Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi. Dziko lapansi ndipo linali lopanda kanthu; ndipo mdima unali pamwamba pa nyanja; ndipo mzimu wa Mulungu unalinkufungatira pamwamba pa madzi. Ndipo anati Mulungu, Kuyere; ndipo kunayera. Ndipo anaona Mulungu kuti kuyerako kunali kwabwino; ndipo Mulungu analekanitsa kuyera ndi mdima. Ndipo Mulungu anacha kuyerako Usana, ndi mdimawo anautcha Usiku. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku loyamba. Ndipo anati Mulungu, Pakhale thambo pakati pamadzi, lilekanitse madzi ndi madzi. Ndipo Mulungu anapanga thambo, nalekanitsa madzi anali pansi pa thambolo ndi madzi anali pamwamba pa thambolo; ndipo kunatero. Ndipo Mulungu analitcha thambolo Kumwamba. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachiwiri. Ndipo anati Mulungu, Madzi a pansi pa kumwamba asonkhane pamodzi pa malo amodzi, uoneke mtunda: ndipo kunatero. Ndipo Mulungu adautcha mtundawo Dziko lapansi; kusonkhana kwa madziko ndipo adatcha Nyanja: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino. Mulungu ndipo anati, Dziko lapansi limere udzu, therere lobala mbeu, ndi mtengo wazipatso wakubala zipatso monga mwa mtundu wake, momwemo muli mbeu yake, pa dziko lapansi: ndipo kunatero. Ndipo dziko lapansi linamera udzu, therere lobala mbeu monga mwa mtundu wake, ndi mtengo wakubala zipatso, momwemo muli mbeu yake, monga mwa mtundu wake; ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachitatu. Ndipo Mulungu anati, Pakhale zounikira pa thambo la kumwamba, zakulekanitsa usana ndi usiku; zikhale zizindikiro ndi nyengo, ndi masiku, ndi zaka; Zikhale zounikira m'thambo la kumwamba, kuti ziunikire pa dziko lapansi: ndipo kunatero. Ndipo Mulungu anapanga zounikira zazikulu ziwiri; chounikira chachikulu chakulamulira usana, chounikira chaching'ono chakulamulira usiku, ndi nyenyezi zomwe. Mulungu ndipo adaika zimenezo m'thambo la kumwamba, kuti ziunikire pa dziko lapansi. Nizilamulire usana ndi usiku, nizilekanitse kuyera ndi mdima: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachinai. Ndipo anati Mulungu, Madzi abale zochuluka zamoyo zoyendayenda, ndi mbalame ziuluke pamwamba pa dziko lapansi ndi pamlengalenga. Mulungu ndipo adalenga zinsomba zazikulu ndi zoyendayenda zamoyo zakuchuluka m'madzi mwa mitundu yao, ndi mbalame zamapiko, yonse monga mwa mtundu wake: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino. Mulungu ndipo anadalitsa zimenezo, nati, Zibalane, zichuluke, zidzaze madzi a m'nyanja, ndi mbalame zichuluke pa dziko lapansi. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachisanu. Ndipo adati Mulungu, Dziko lapansi libale zamoyo monga mwa mitundu yao, ng'ombe, ndi zokwawa, ndi zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao: ndipo kunatero. Ndipo Mulungu anapanga zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao; ndi ng'ombe monga mwa mtundu wake, ndi zonse zokwawa pansi monga mwa mitundu yao; ndipo Mulungu anaona kuti kunali kwabwino. Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m'chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu: alamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi pa ng'ombe, ndi pa dziko lonse lapansi, ndi pa zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi. Mulungu ndipo adalenga munthu m'chifanizo chake, m'chifanizo cha Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi. Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi. Ndipo anati Mulungu, Taonani, ndakupatsani inu therere lonse lakubala mbeu lili pa dziko lapansi, ndi mitengo yonse m'mene muli chipatso cha mtengo wakubala mbeu; chidzakhala chakudya cha inu: ndiponso ndapatsa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi zakukwawa zonse za dziko lapansi m'mene muli moyo, therere laliwisi lonse likhale chakudya: ndipo kunatero. Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi. Ndipo zinatha kupangidwa zakumwamba ndi dziko lapansi, ndi khamu lao lonse. Tsiku lachisanu ndi chiwiri Mulungu anamaliza ntchito yonse anaipanga; ndipo anapuma tsiku lachisanu ndi chiwiri ku ntchito yake yonse. Mulungu ndipo anadalitsa tsiku lachisanu ndi chiwiri, naliyeretsa limenelo: chifukwa limenelo adapuma ku ntchito yake yonse imene Mulungu anailenga ndi kupanga. Imeneyo ndiyo mibadwo yao ya zakumwamba ndi dziko lapansi, pamene zinalengedwa, tsiku lomwe Yehova Mulungu anapanga dziko lapansi ndi zakumwamba. Ndi zomera zonse za m'munda zisanakhale m'dziko lapansi, ndiponso matherere onse a m'munda asanamere; chifukwa Yehova Mulungu sanavumbitsire mvula pa dziko lapansi, ndipo panalibe munthu wakulima nthaka; koma inakwera nkhungu yotuluka pa dziko lapansi, niithirira ponse pamwamba pa nthaka. Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m'mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo. Ndipo Yehova Mulungu anabzala m'munda ku Edeni chakum'mawa; momwemo ndipo adaika munthu adamuumbayo. Ndipo Yehova Mulungu anameretsa m'nthaka mitengo yonse yokoma m'maso ndi yabwino kudya; ndiponso mtengo wa moyo pakati pa mundapo, ndi mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa. Ndipo unatuluka m'Edeni mtsinje wakuthirira m'mundamo, m'menemo ndipo unalekana nuchita miyendo inai. Dzina la wakuyamba Pisoni: umenewo ndiwo wozungulira dziko lonse la Havila, m'mene muli golide; golide wa dziko ali wabwino; ndimonso muli bedola ndi mwala wasohamu. Dzina la mtsinje wachiwiri ndi Gihoni: umenewo ndiwo wozungulira dziko lonse la Kusi. Dzina la mtsinje wachitatu ndi Tigrisi: umenewo ndiwo wakuyenda cha kum'mawa kwake kwa Asiriya. Mtsinje wachinai ndi Yufurate. Ndipo Yehova Mulungu anatenga munthuyo, namuika iye m'munda wa Edeni kuti aulime nauyang'anire. Ndipo Yehova Mulungu anamuuza munthuyo, nati, Mitengo yonse ya m'munda udyeko; koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu. Yehova Mulungu ndipo anati, Si kwabwino kuti munthu akhale yekha; ndidzampangira womthangatira iye. Ndipo Yehova Mulungu anaumba ndi nthaka zamoyo zonse za m'thengo, ndi mbalame zonse za m'mlengalenga; ndipo anapita nazo kwa Adamu kuti aone maina omwe adzazicha; ndipo maina omwe onse anazicha Adamu zamoyo zonse, omwewo ndiwo maina ao. Adamu ndipo anazitcha maina zinyama zonse, ndi mbalame za m'mlengalenga ndi zamoyo zonse za m'thengo: koma kwa Adamu sanapezedwa womthangatira iye. Koma Yehova Mulungu anamgonetsa Adamu tulo tatikulu, ndipo anagona; ndipo anatengako nthiti yake imodzi, natsekapo ndi mnofu pamalo pake. Ndipo nthitiyo anaichotsa Yehova Mulungu mwa Adamu anaipanga mkazi, ndipo ananka naye kwa Adamu. Ndipo anati Adamu, Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga, ndi mnofu wa mnofu wanga; ndipo adzatchedwa Mkazi, chifukwa anamtenga mwa mwamuna. Chifukwa chotero mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi. Onse awiri ndipo anali amaliseche, mwamuna ndi mkazi wake, ndipo analibe manyazi. Ndipo njoka inali yakuchenjera yoposa zamoyo zonse za m'thengo zimene anazipanga Yehova Mulungu. Ndipo inati kwa mkaziyo, Eya! Kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m'mundamu? Mkaziyo ndipo anati kwa njoka, Zipatso za mitengo ya m'mundamu tidye. Koma zipatso za mtengo umene uli m'kati mwa munda, Mulungu anati, Musadye umenewo, musakhudze umenewo, mungadzafe. Njokayo ndipo inati kwa mkaziyo, Kufa simudzafai; chifukwa adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa. Ndipo pamene anaona mkaziyo kuti mtengo unali wabwino kudya, ndi kuti unali wokoma m'maso, mtengo wolakalakika wakupatsa nzeru, anatenga zipatso zake, nadya, napatsanso mwamuna wake amene ali naye, nadya iyenso. Ndipo anatseguka maso ao a onse awiri, nadziwa kuti anali amaliseche: ndipo adasoka masamba amkuyu, nadzipangira matewera. Ndipo anamva mau a Yehova Mulungu alinkuyendayenda m'munda nthawi yamadzulo: ndipo anabisala Adamu ndi mkazi wake pamaso pa Yehova Mulungu pakati pa mitengo ya m'munda. Ndipo Yehova Mulungu anaitana mwamunayo nati kwa iye, Uli kuti? Ndipo anati, Ndinamva mau anu m'mundamu, ndipo ndinaopa chifukwa ndinali wamaliseche ine; ndipo ndinabisala. Ndipo anati, Ndani anakuuza iwe kuti uli wamaliseche? Kodi wadya za mtengo uja, umene ndinakuuza iwe kuti usadye? Ndipo anati mwamunayo, Mkazi amene munandipatsa ine kuti akhale ndi ine, ameneyo anandipatsa ine za mtengo, ndipo ndinadya. Ndipo Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, Chiyani chimene wachitachi? Ndipo anati mkaziyo, Njoka inandinyenga ine, ndipo ndinadya. Ndipo anati Yehova Mulungu kwa njokayo, Chifukwa kuti wachita ichi, wotembereredwa ndiwe wopambana ndi zinyama zonse ndi zamoyo zonse za m'thengo: uziyenda ndi pamimba pako, uzidya fumbi masiku onse a moyo wako: ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake. Kwa mkaziyo ndipo anati, Ndidzachulukitsa kusauka kwako ndi potenga mimba pako; udzasauka pakubala: udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe. Kwa Adamu ndipo anati, Chifukwa kuti wamvera mau a mkazi wako, nudya za mtengo umene ndinakuuza iwe kuti, Usadyeko; nthaka ikhale yotembereredwa chifukwa cha iwe; m'kusauka udzadyako masiku onse a moyo wako: minga ndi mitula idzakubalira iwe; ndipo udzadya therere la m'thengo: m'thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti m'menemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera. Ndipo mwamuna anamutcha dzina la mkazi wake, Heva; chifukwa ndiye amake wa amoyo onse. Yehova Mulungu ndipo anapangira Adamu ndi mkazi wake malaya azikopa, nawaveka iwo. Ndipo anati Yehova Mulungu, Taonani, munthuyo akhala ngati mmodzi wa ife, wakudziwa zabwino ndi zoipa: ndipo tsopano kuti asatambasule dzanja lake ndi kutenga za mtengo wa moyo, ndi kudya, ndi kukhala ndi moyo nthawi zonse, Yehova Mulungu anamtulutsa iye m'munda wa Edeni, kuti alime nthaka m'mene anamtenga iye. Ndipo anamuingitsa munthuyo; nakhazika akerubi cha kum'mawa kwake kwa munda wa Edeni, ndi lupanga lamoto lakuzungulira ponsepo, lakusunga njira ya ku mtengo wa moyo. Ndipo mwamunayo anadziwa mkazi wake Heva: ndipo anatenga pakati, nabala Kaini, ndipo anati, Ndalandira munthu kwa Yehova. Ndipo anabalanso mphwake Abele. Abele anakhala mbusa wa nkhosa, koma Kaini anali wakulima nthaka. Ndipo panali atapita masiku, Kaini anatenga zipatso za nthaka, nsembe ya kwa Yehova. Ndiponso Abele anatenga iyenso mwana woyamba wa nkhosa zake ndi mafuta omwe. Yehova ndipo anayang'anira Abele ndi nsembe yake: koma sanayang'anire Kaini ndi nsembe yake. Kaini ndipo anakwiya kwambiri, niigwa nkhope yake. Ndipo Yehova anati kwa Kaini, Ukwiyiranji? Yagweranji nkhope yako? Ukachita zabwino, sudzalandiridwa kodi? Ukaleka kuchita zabwino, uchimo ubwatama pakhomo: kwa iwe kudzakhala kulakalaka kwake, ndipo iwe udzamlamulira iye. Kaini ndipo ananena ndi Abele mphwake. Ndipo panali pamene anali kumunda, Kaini anamuukira Abele mphwake, namupha. Yehova ndipo anati kwa Kaini, Ali kuti Abele mphwako? Ndipo anati, Sindidziwai: kodi ndine woyang'anira mphwanga? Ndipo anati, Wachita chiyani? Mau a mwazi wa mphwako andifuulira Ine kunthaka. Tsopano ndiwe wotembereredwa kunthaka, imene inatsegula pakamwa pake kulandira pa dzanja lako mwazi wa mphwako: pamene udzalima panthaka siidzaperekanso kwa iwe mphamvu yake: udzakhala wothawathawa ndi woyendayenda pa dziko lapansi. Ndipo Kaini anati kwa Yehova, Kulangidwa kwanga nkwakukulu kosapiririka. Taonani, mwandiingitsa ine lero lomwe padziko; ndi pankhope panu ndidzabisika; ndipo ndidzakhala wothawathawa ndi woyendayenda pa dziko lapansi; ndipo kudzatero kuti onse akundipeza adzandipha. Ndipo Yehova anati kwa iye, Chifukwa chake aliyense amene adzapha Kaini kudzabwezedwa kwa iye kasanu ndi kawiri. Ndipo Yehova anaika chizindikiro pa Kaini, kuti asamuphe aliyense akampeza. Ndipo Kaini anatuluka pamaso pa Yehova, ndipo anakhala m'dziko la Nodi, kum'mawa kwake kwa Edeni. Ndipo Kaini anamdziwa mkazi wake; ndipo anatenga pakati, nabala Enoki: ndipo anamanga mudzi, nautcha dzina lake la mudziwo monga dzina la mwana wake, Enoki. Kwa Enoki ndipo kunabadwa Iradi; Iradi ndipo anabala Mehuyaele; Mehuyaele ndipo anabala Metusaele; Metusaele ndipo anabala Lameki. Ndipo Lameki anadzitengera yekha akazi awiri: dzina lake la wina ndi Ada, dzina lake la mnzake ndi Zila. Ndipo Ada anabala Yabala; iye ndiye atate wao wa iwo okhala m'mahema, akuweta ng'ombe. Ndi dzina la mphwake ndilo Yubale; iye ndiye atate wao wa iwo oimba zeze ndi chitoliro. Ndipo Zila, iyenso anabala Tubala-Kaini, mwini wakuphunzitsa amisiri onse a mkuwa ndi a chitsulo; mlongo wake wa Tubala-Kaini ndi Naama. Lameki ndipo anati kwa akazi ake, Tamvani mau anga, Ada ndi Zila; inu akazi a Lameki, mverani kunena kwanga: Ndapha munthu wakundilasa ine, ndapha mnyamata wakundipweteka ine. Ngati Kaini adzabwezeredwa kasanu ndi kawiri, koma Lameki makumi asanu ndi awiri. Ndipo Adamu anadziwanso mkazi wake; ndipo anabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Seti: Chifukwa, nati iye, Mulungu wandilowezera ine mbeu ina m'malo mwa Abele amene Kaini anamupha. Ndiponso kwa Seti, kwa iye kunabadwa mwana wamwamuna: anamutcha dzina lake Enosi: pomwepo anthu anayamba kutchula dzina la Yehova. Ili ndi buku la mibadwo ya Adamu. Tsiku lomwe Mulungu analenga munthu anamlenga m'chifanizo cha Mulungu; anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi, nawadalitsa iwo natcha mtundu wao anthu, tsiku lomwe anawalenga iwo. Ndipo Adamu anakhala ndi moyo zaka zana limodzi kudza makumi atatu, nabala mwana wamwamuna m'chifanizo chake; namutcha dzina lake Seti. Masiku ake Adamu atabala Seti, anali zaka mazana asanu ndi atatu; ndipo anabala ana aamuna ndi aakazi. Masiku ake onse anakhala ndi moyo Adamu anali zaka mazana asanu ndi anai, kudza makumi atatu; ndipo anamwalira. Ndipo Seti anakhala ndi moyo zaka zana kudza zisanu, nabala Enosi; ndipo Seti anakhala ndi moyo, atabala Enosi, zaka mazana asanu ndi atatu kudza zisanu ndi ziwiri: ndipo anabala ana aamuna ndi aakazi: masiku ake onse a Seti anali zaka mazana asanu ndi anai kudza khumi ndi ziwiri; ndipo anamwalira. Ndipo Enosi anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi anai, nabala Kenani; ndipo anakhala ndi moyo Enosi, atabala Kenani, zaka mazana asanu ndi atatu kudza khumi ndi zisanu: ndipo anabala ana aamuna ndi aakazi. Masiku ake onse a Enosi anali mazana asanu ndi anai kudza zisanu; ndipo anamwalira. Ndipo Kenani anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi awiri, ndipo anabala Mahalalele: ndipo Kenani anakhala ndi moyo, atabala Mahalalele zaka mazana asanu ndi atatu kudza makumi anai, ndipo anabala ana aamuna ndi aakazi; masiku ake onse a Kenani anali zaka mazana asanu ndi anai kudza khumi; ndipo anamwalira. Ndipo Mahalalele anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu, nabala Yaredi; ndipo Mahalalele anakhala ndi moyo, atabala Yaredi, zaka mazana asanu ndi atatu kudza makumi atatu, nabala ana aamuna ndi aakazi: masiku ake onse a Mahalalele anali zaka mazana asanu ndi atatu kudza makumi asanu ndi anai ndi zisanu; ndipo anamwalira. Ndipo Yaredi anakhala ndi moyo zaka zana kudza makumi asanu ndi limodzi ndi ziwiri, nabala Enoki; ndipo Yaredi anakhala ndi moyo, atabala Enoki, zaka mazana asanu ndi atatu, nabala ana aamuna ndi aakazi; masiku ake onse a Yaredi anali zaka mazana asanu ndi anai kudza makumi asanu ndi limodzi ndi ziwiri: ndipo anamwalira. Ndipo Enoki anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu, nabala Metusela: ndipo Enoki anayendabe ndi Mulungu, atabala Metusela, zaka mazana atatu, nabala ana aamuna ndi aakazi; masiku ake onse a Enoki anali mazana atatu kudza makumi asanu ndi limodzi ndi zisanu; ndipo Enoki anayendabe ndi Mulungu; ndipo panalibe iye; pakuti Mulungu anamtenga. Ndipo Metusela anakhala ndi moyo zaka zana kudza makumi asanu ndi atatu ndi zisanu ndi ziwiri, nabala Lameki; ndipo Metusela anakhala ndi moyo, atabala Lameki, zaka mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi atatu ndi awiri, nabala ana aamuna ndi aakazi: masiku ake onse a Metusela anali mazana asanu ndi anai kudza makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu ndi zinai; ndipo anamwalira. Ndipo Lameki anakhala ndi moyo zaka zana kudza makumi asanu ndi atatu ndi ziwiri, nabala mwana wamwamuna; namutcha dzina lake Nowa, ndi kuti, Yemweyu adzatonthoza mtima wathu pa ntchito zathu zovuta za manja athu, chifukwa cha nthaka imene anaitemberera Yehova; ndipo Lameki anakhala ndi moyo atabala Nowa, zaka mazana asanu kudza makumi asanu ndi anai ndi zisanu, nabala ana aamuna ndi aakazi: masiku ake onse a Lameki anali zaka mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi awiri; ndipo anamwalira. Ndipo Nowa anali wa zaka mazana asanu; ndipo Nowa anabala Semu ndi Hamu ndi Yafeti. Ndipo panali pamene anthu anayamba kuchuluka padziko, ndi ana akazi anawabadwira iwo, kuti ana amuna a Mulungu anayang'ana ana akazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha. Ndipo anati Yehova, Mzimu wanga sudzakangana ndi anthu nthawi zonse, chifukwa iwonso ndiwo thupi lanyama: koma masiku ake adzakhala zaka zana limodzi kudza makumi awiri. Pa dziko lapansi panali anthu akulukulu masiku omwewo ndiponso pambuyo pake, ana amuna a Mulungu atalowa kwa ana akazi a anthu, ndipo anabalira iwo ana, amenewo ndiwo anthu amphamvu akalekale, anthu omveka. Ndipo anaona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukulu pa dziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yao zinali zoipabe zokhazokha. Ndipo Yehova anamva chisoni chifukwa anapanga munthu pa dziko lapansi, ndipo anavutika m'mtima mwake. Ndipo anati Yehova, Ndidzafafaniza anthu amene ndawalenga pa dziko lapansi; anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga: pakuti ndimva chisoni chifukwa ndapanga izo. Koma Nowa anapeza ufulu pamaso pa Yehova. Mibadwo ya Nowa ndi iyi: Nowa anali munthu wolungama ndi wangwiro m'mibadwo yake; Nowa anayendabe ndi Mulungu. Ndipo Nowa anabala ana amuna atatu, Semu, Hamu ndi Yafeti. Ndipo dziko lapansi linavunda pamaso pa Mulungu, dziko lapansi ndipo linadzala ndi chiwawa. Ndipo Mulungu anaona dziko lapansi, ndipo taonani, linavunda; pakuti anthu onse anavunditsa njira yao pa dziko lapansi. Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Chimaliziro chake cha anthu onse chafika pamaso panga; pakuti dziko lapansi ladzala ndi chiwawa chifukwa cha iwo; taonani, ndidzaononga iwo pamodzi ndi dziko lapansi. Udzipangire wekha chingalawa cha mtengo wanjale; upangemo zipinda m'chingalawamo, ndipo upake ndi utoto m'kati ndi kunja. Kupanga kwake ndi kotere: m'litali mwake mwa chingalawa mikono mazana atatu, m'mimba mwake mikono makumi asanu, m'msinkhu mwake mikono makumi atatu. Uike zenera m'chingalawacho, ulimalize ndi kusiya mkono umodzi pamwamba pake: khomo la chingalawa uike m'mbali mwake; nuchipange ndi nyumba yapansi, ndi yachiwiri, ndi yachitatu. Ndine, taonani, ndipo Ine ndidzadzetsa chigumula cha madzi pa dziko lapansi, kuti chiononge zamoyo zonse, m'mene muli mpweya wa moyo pansi pa thambo; zinthu zonse za m'dziko lapansi zidzafa. Koma ndidzakhazikitsa ndi iwe pangano langa; ndipo udzalowa m'chingalawamo iwe ndi ana ako ndi mkazi wako, ndi akazi a ana ako pamodzi ndi iwe. Ndipo zonse zokhala ndi moyo, ziwiriziwiri za mtundu wao ulowetse m'chingalawamo, kuti zikhale ndi moyo pamodzi ndi iwe; zikhale zamphongo ndi zazikazi. Za mbalame monga mwa mitundu yao, ndi zinyama monga mwa mitundu yao, ndi zokwawa zonse za dziko lapansi monga mwa mitundu yao, ziwiriziwiri monga mwa mitundu yao, zidzadza kwa iwe kuti zikhale ndi moyo. Ndipo iwe udzitengereko wekha zakudya zonse zodyedwa, nudzisonkhanitsire izi wekha: ndipo zidzakhala zakudya za iwe ndi za iwo. Chotero anachita Nowa, monga mwa zonse anamlamulira iye Mulungu, momwemo anachita. Ndipo anati Yehova kwa Nowa, Talowani, iwe ndi akunyumba ako onse m'chingalawamo; chifukwa ndakuona iwe kuti uli wolungama pamaso panga m'mbadwo uno. Nyama zonse zodyedwa udzitengereko wekha zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri, yamphongo ndi yaikazi yake; ndi nyama zosadyedwa ziwiriziwiri yamphongo ndi yaikazi yake. Ndiponso mbalame za kumlengalenga zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri, yaimuna ndi yaikazi, kuti mbeu ikhale ndi moyo pa dziko lonse lapansi. Pakuti akapita masiku asanu ndi awiri Ine ndidzavumbitsa mvula pa dziko lapansi masiku makumi anai usana ndi usiku; ndi zinthu zamoyo zonse zomwe ndazipanga ndidzaziononga pa dziko lapansi. Ndipo anachita Nowa monga mwa zonse anamlamulira iye Yehova. Ndipo Nowa anali wa zaka mazana asanu ndi limodzi, pamene chigumula cha madzi chinali pa dziko lapansi. Ndipo analowa Nowa ndi ana ake ndi mkazi wake ndi akazi a ana ake m'chingalawamo, chifukwa cha madzi a chigumula. Nyama zodyedwa ndi nyama zosadyedwa, ndi mbalame, ndi zonse zokwawa pansi, zinalowa ziwiriziwiri kwa Nowa m'chingalawamo, yamphongo ndi yaikazi, monga momwe Mulungu anamlamulira Nowa. Ndipo panali pamene anapita masiku asanu ndi awiri, madzi a chigumula anali pa dziko lapansi. Chaka cha mazana asanu ndi limodzi cha moyo wa Nowa, mwezi wachiwiri, tsiku la khumi ndi asanu ndi awiri la mwezi, tsiku lomwelo akasupe onse a madzi aakulu anasefuka, ndi mazenera a kumwamba anatseguka. Ndipo mvula inali pa dziko lapansi masiku makumi anai usana ndi usiku. Tsiku lomwelo analowa m'chingalawamo Nowa, ndi Semu, ndi Hamu, ndi Yafeti, ana a Nowa, ndi mkazi wake wa Nowa, ndi akazi atatu a ana ake pamodzi nao: iwo, ndi zamoyo zonse monga mwa mitundu yao, ndi zinyama zonse monga mwa mitundu yao, zokwawa zonse zokwawa pa dziko lapansi monga mwa mitundu yao, ndi zouluka zonse monga mwa mitundu yao, ndi mbalame zonse za mitundumitundu. Ndipo zinalowa kwa Nowa m'chingalawamo ziwiriziwiri zamoyo zonse, m'mene muli mpweya wa moyo. Zimene zinalowazo, zinalowa yamphongo ndi yaikazi zamoyo zonse, monga momwe Mulungu anamlamulira iye: ndipo Yehova anamtsekera iye. Ndipo chigumula chinali pa dziko lapansi masiku makumi anai: ndipo madzi anachuluka natukula chingalawa, ndipo chinakwera pamwamba pa dziko lapansi. Ndipo madzi anapambana, nachuluka ndithu pa dziko lapansi, ndipo chingalawa chinayandama pamadzi. Ndipo madzi anapambana ndithu pa dziko lapansi; anamizidwa mapiri aatali onse amene anali pansi pa thambo lonse. Madzi anapambana ndithu nakwera mikono khumi ndi isanu: namizidwa mapiri. Ndipo zinafa zamoyo zonse zoyenda pa dziko lapansi, zouluka, ndi nyama, ndi zamoyo, ndi zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi, ndi anthu onse: zonse zimene m'mphuno zao munali mpweya wa mzimu wa moyo, zonse zinali pamtunda, zinafa. Ndipo zinaonongedwa zamoyo zonse zimene zinali pa dziko lapansi, anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga; ndipo zinaonongedwa pa dziko lapansi: anatsala Nowa yekha ndi amene anali pamodzi naye m'chingalawa. Ndipo anapambana madzi pa dziko lapansi masiku zana kudza makumi asanu. Ndipo Mulungu anakumbukira Nowa ndi zamoyo zonse, ndi nyama zonse zimene zinali pamodzi naye m'chingalawamo; ndipo Mulungu anapititsa mphepo pa dziko lapansi, naphwa madzi; ndipo anatsekedwa akasupe a madzi aakulu ndi mazenera a kumwamba, niletsedwa mvula ya kumwamba; ndipo madzi anaphweraphwerabe pa dziko lapansi: pamene anatha masiku zana limodzi kudza makumi atatu madzi anachepa. Ndipo chingalawa chinaima pa mapiri a Ararati, mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi ndi asanu ndi awiri la mwezi. Ndipo madzi analinkuchepa kufikira mwezi wakhumi; mwezi wakhumi tsiku loyamba mwezi ndipo padaoneka mitu ya mapiri. Ndipo panali atapita masiku makumi anai, Nowa anatsegula pa zenera la chingalawa limene analipanga: ndipo anatulutsa khungubwi, ndipo anatuluka kunka kwina ndi kwina kufikira adaphwa madzi pa dziko lapansi. Ndipo anatulutsa njiwa imchokere, kuti aone kapena madzi anaphwa pamwamba pa dziko lapansi; koma njiwayo siinapeza popondapo phazi lake, nibwera kwa iye kuchingalawako, pakuti madzi analipo pa dziko lonse lapansi; ndipo anatulutsa dzanja lake, naitenga, nailowetsa kwa iye m'chingalawamo. Ndipo analinda masiku ena asanu ndi awiri; natulutsanso njiwayo m'chingalawamo; ndipo njiwa inadza kwa iye madzulo; ndipo, taonani, m'kamwa mwake munali tsamba la azitona lothyoledwa: ndipo anadziwa Nowa kuti madzi analimkuphwa pa dziko lapansi. Ndipo analindanso masiku ena asanu ndi awiri; natulutsa njiwayo: ndipo siinabweranso konse kwa iye. Ndipo panali chaka cha mazana asanu ndi limodzi kudza chimodzi, mwezi woyamba, tsiku loyamba mwezi, madzi anaphwa pa dziko lapansi; ndipo Nowa anachotsa chindwi lake pachingalawa, nayang'ana, ndipo taonani, padauma pa dziko lapansi. Mwezi wachiwiri tsiku la makumi awiri kudza asanu ndi awiri la mwezi, lidauma dziko lapansi. Mulungu ndipo ananena kwa Nowa, kuti, Tulukamoni m'chingalawamo, iwe ndi ana ako, ndi mkazi wako, ndi akazi a ana ako pamodzi ndi iwe. Tulutsa pamodzi ndi iwe zamoyo zonse zili ndi iwe za nyama zonse, zouluka, ndi zinyama, ndi zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi; kuti ziswane pa dziko lapansi, zibalane, zichuluke pa dziko lapansi, zibalane, zichuluke pa dziko lapansi. Ndipo anatuluka Nowa ndi ana ake, ndi mkazi wake, ndi akazi a ana ake, pamodzi naye: zinyama zonse, zokwawa zonse, zouluka zonse, ndi zonse zokwawa pa dziko lapansi, monga mwa mitundu yao, zinatuluka m'chingalawamo. Ndipo Nowa anamanga guwa la nsembe la Yehova; natengapo nyama zodyedwa zonse ndi mbalame zodyedwa zonse napereka nsembe zopsereza paguwapo. Ndipo Yehova anamva chonunkhira chakukondweretsa; nati Yehova m'mtima mwake, Sindidzatembereranso konse nthaka chifukwa cha munthu; pakuti ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake; sindidzaphanso konse zinthu zonse zamoyo, monga momwe ndachitiramo. Pakukhalabe masiku a dziko lapansi, nthawi yakubzala ndi yakukunkha, chisanu ndi mafundi, malimwe ndi msakasa, usana ndi usiku sizidzalekai. Ndipo Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake, nati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi. Kuopsa kwanu, ndi kuchititsa mantha kwanu kudzakhala pa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi pa zouluka zonse za m'mlengalenga; ndi pa zonse za m'nyanja, zapatsidwa m'dzanja lanu. Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; monga therere laliwisi ndakupatsani inu zonsezo. Koma nyama, m'mene muli moyo wake, ndiwo mwazi wake, musadye. Zoonatu mwazi wanu wa miyoyo yanu ndidzafuna; pa dzanja la zinyama zonse ndidzaufuna: ndi pa dzanja la munthu, pa dzanja la mbale wake wa munthu ndidzaufuna moyo wa munthu. Amene akhetsa mwazi wa munthu, ndi munthunso mwazi wake udzakhetsedwa: chifukwa m'chifanizo cha Mulungu Iye anampanga munthu. Ndi inu, mubalane, muchuluke; muswane pa dziko lapansi, nimuchuluke m'menemo. Ndipo Mulungu ananena kwa Nowa ndi kwa ana ake pamodzi naye, kuti, Ndipo Ine, taonani, Ine ndikhazikitsa pangano langa pamodzi ndi inu, ndi mbeu zanu pambuyo panu; ndi zamoyo zonse zili pamodzi ndi inu, zouluka, ng'ombe, ndi zinyama zonse za dziko lapansi, pamodzi ndi inu; zonse zotuluka m'chingalawa, zinyama zonse za dziko lapansi. Ndipo ndidzakhazikitsa pangano langa pamodzi ndi inu; zamoyo zonse sizidzamalizidwanso konse ndi madzi a chigumula; ndipo sikudzakhalanso konse chigumula cha kuononga dziko lapansi. Ndipo anati Mulungu, Ichi ndichi chizindikiro cha pangano limene ndipangana ndi Ine ndi inu, ndi zamoyo zonse zili pamodzi ndi inu, ku mibadwomibadwo; ndiika utawaleza wanga m'mtambomo, ndipo udzakhala chizindikiro cha pangano lopangana ndi Ine ndi dziko lapansi. Ndipo padzakhala pophimba ndi mtambo Ine dziko lapansi, utawo udzaoneka m'mtambomo; ndipo ndidzakumbukira pangano langa limene lili ndi Ine ndi inu, ndi zamoyo zonse zokhala ndi moyo; ndipo madzi sadzakhalanso konse chigumula chakuononga zamoyo zonse. Ndipo utawo udzakhala m'mtambo; ndipo ndidzauyang'anira kuti ndikumbukire pangano lachikhalire lili ndi Mulungu ndi zamoyo zonse zokhala ndi moyo pa dziko lapansi. Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Ichi ndichi chizindikiro cha pangano ndalikhazikitsa popangana ndi Ine ndi zamoyo zonse za pa dziko lapansi. Ndi ana amuna a Nowa amene anatuluka m'chingalawa ndiwo Semu, ndi Hamu, ndi Yafeti: Hamu ndiye atate wake wa Kanani. Amenewa ndiwo ana amuna atatu a Nowa: ndiwo anafalikira dziko lonse lapansi. Ndipo anayamba Nowa kukhala munthu wakulima nthaka, ndipo analima munda wamphesa: namwa vinyo wake, naledzera; ndipo anali wamaliseche m'kati mwa hema wake. Ndipo Hamu atate wake wa Kanani, anauona umaliseche wa atate wake, nauza abale ake awiri amene anali kunja. Semu ndi Yafeti ndipo anatenga chofunda, nachiika pa mapewa ao a onse awiri, nayenda chambuyo, nafunditsa umaliseche wa atate wao: nkhope zao zinali chambuyo, osaona umaliseche wa atate ao. Nowa ndipo anauka kwa kuledzera kwake, nadziwa chimene anamchitira iye mwana wake wamng'ono. Ndipo anati, Wotembereredwa ndi Kanani; adzakhala kwa abale ake kapolo wa akapolo. Ndipo anati, Ayamikike Yehova, Mulungu wa Semu; Kanani akhale kapolo wake. Mulungu akuze Yafeti, akhale iye m'mahema a Semu; Kanani akhale kapolo wake. Ndipo Nowa anakhala ndi moyo chigumula chitapita, zaka mazana atatu kudza makumi asanu. Ndipo masiku onse a Nowa anali mazana asanu ndi anai kudza makumi asanu: ndipo anamwalira. Mibadwo ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti, ndi iyi; kwa iwo ndipo kunabadwa ana amuna, chitapita chigumula chija. Ana amuna a Yafeti: Gomeri, ndi Magogi, ndi Madai, ndi Yavani, ndi Tubala, ndi Meseki ndi Tirasi. Ndi ana amuna a Gomeri: Asikenazi, ndi Rifati, ndi Togarima. Ndi ana amuna a Yavani: Elisa, ndi Tarisisi, ndi Kitimu, ndi Dodanimu. Amenewo ndipo anagawa zisi za amitundu m'maiko mwao, onse amene monga mwa chinenedwe chao; ndi mwa mabanja ao, ndi m'mitundu yao. Ndi ana amuna a Hamu: Kusi, ndi Ejipito, ndi Puti, ndi Kanani. Ndi ana amuna a Kusi: Seba, ndi Havila, ndi Sabita, ndi Raama, ndi Sabiteka; ndi ana a Raama: Sheba ndi Dedani. Ndipo Kusi anabala Nimirodi; ndipo iye anayamba kukhala wamphamvu pa dziko lapansi. Iye ndiye mpalu wamphamvu pamaso pa Yehova: chifukwa chake kunanenedwa, Monga Nimirodi mpalu wamphamvu pamaso pa Yehova. Ndipo kuyamba kwake kwa ufumu wake kunali Babiloni, ndi Ereke, ndi Akadi, ndi Kaline, m'dziko la Sinara. M'dziko momwemo iye anatuluka kunka ku Asiriya, namanga Ninive, ndi mudzi wa Rehoboti, ndi Kala, ndi Reseni pakati pa Ninive ndi Kala: umenewo ndi mudzi waukulu. Ejipito ndipo anabala Ludimu, ndi Anamimu, ndi Lehabu, ndi Nafituhimu, ndi Patirusimu, ndi Kasiluhimu, m'menemo ndipo anatuluka Afilisti, ndi Kafitori. Ndipo Kanani anabala Sidoni woyamba wake, ndi Heti: ndi Ayebusi, ndi Aamori, ndi Agirigasi; ndi Ahivi, ndi Aariki, ndi Asini; ndi Aaravadi, ndi Aazemari, ndi Ahamati; pambuyo pake pamenepo ndipo mabanja a Akanani anafalikira. Ndipo malire a Akanani anayamba pa Sidoni, pakunka ku Gerari ndi ku Gaza; pakunka ku Sodomu, ndi ku Gomora, ndi Adima, ndi Zeboimu, kufikira ku Lasa. Amenewa ndi ana amuna a Hamu monga mwa mabanja ao, mwa zinenedwe zao, m'maiko ao, m'mitundu yao. Ndiponso kwa Semu atate wa ana onse a Eberi, mkulu wa Yafeti, kwa iye kunabadwa ana. Ana amuna a Semu; Elamu, ndi Asiriya, ndi Aripakisadi, ndi Ludi, ndi Aramu. Ndi ana a Aramu: Uzi ndi Huli ndi Getere, ndi Masi. Aripakisadi ndipo anabala Sela; ndipo Sela anabala Eberi. Kwa Eberi ndipo kunabadwa ana amuna awiri; dzina la wina ndi Pelegi; chifukwa kuti m'masiku ake dziko lapansi linagawanikana; dzina la mphwake ndi Yokotani. Ndipo Yokotani anabala Alimodadi, ndi Selefi, ndi Hazara-Maveti, ndi Yera; ndi Hadoramu ndi Uzali, ndi Dikila; ndi Obala, ndi Abimaele, ndi Sheba; ndi Ofiri ndi Havila, ndi Yobabu; onse amenewa ndi ana a Yokotani. Kwao kunayamba pa Mesa pakunka ku Sefari phiri la kum'mawa. Amenewa ndi ana a Semu, monga mwa mabanja ao, mwa zinenedwe zao, m'maiko ao, m'mitundu yao. Amenewo ndi mabanja a ana a Nowa monga mwa mibadwo yao, m'mitundu yao: ndi amenewo anagawanika mitundu pa dziko lapansi, chitapita chigumula. Ndipo dziko lapansi linali la chinenedwe chimodzi ndi chilankhulidwe chimodzi. Ndipo panali pamene anayendayenda ulendo kum'mawa, anapeza chigwa m'dziko la Sinara, ndipo anakhala kumeneko. Ndipo ananenana wina ndi wina, Tiyeni tipange njerwa, tiziochetse. Ndipo anali ndi njerwa naziyesa miyala, ndi katondo anayesa matope. Ndipo anati, Tiyeni, timange mudzi ndi nsanja, pamutu pake pafikire kumwamba; ndipo tidzipangire ife tokha dzina kuti tisabalalike pa dziko lonse lapansi. Ndipo Yehova anatsikira kudzaona mudzi ndi nsanja imene analinkumanga ana a anthu. Ndipo Yehova anati, Taonani, anthu ali amodzi, ndipo onse ali nacho chinenedwe chao chimodzi; ndipo ichi ayamba kuchita: ndipo tsopano palibe kanthu kakuletsedwa nao kamene akafuna kuchita. Tiyeni, titsike, pomwepo tisokoneze chinenedwe chao, kuti wina asamvere chinenedwe cha mnzake. Ndipo Yehova anabalalitsa iwo pa dziko lonse lapansi, ndipo analeka kumanga mudzi. Chifukwa chake anatcha dzina lake Babele; pakuti kumeneko Yehova anasokoneza chinenedwe cha dziko lonse lapansi; kuyambira pamenepo Yehova anabalalitsa iwo pa dziko lonse lapansi. Mibadwo ya Semu ndi iyi: Semu anali wa zaka zana limodzi ndipo anabala Aripakisadi, chitapita chigumula zaka ziwiri; ndipo Semu anakhala ndi moyo zaka mazana asanu, atabala Aripakisadi, nabala ana aamuna ndi aakazi. Ndipo Aripakisadi anakhala ndi moyo zaka makumi atatu kudza zisanu nabala Sela; ndipo Aripakisadi anakhala ndi moyo zaka mazana anai kudza zitatu, atabala Sela, nabala ana aamuna ndi aakazi. Ndipo Sela anakhala ndi moyo zaka makumi atatu, nabala Eberi; ndipo Sela anakhala ndi moyo zaka mazana anai kudza zitatu, atabala Eberi, nabala ana aamuna ndi aakazi. Ndipo Eberi anakhala ndi moyo zaka makumi atatu kudza zinai, nabala Pelegi; ndipo Eberi anakhala ndi moyo zaka mazana anai kudza makumi awiri, atabala Pelegi, nabala ana aamuna ndi aakazi. Ndipo Pelegi anakhala ndi moyo zaka makumi atatu, nabala Reu; ndipo Pelegi anakhala ndi moyo zaka mazana awiri kudza zisanu ndi zinai, atabala Reu, nabala ana aamuna ndi aakazi. Ndipo Reu anakhala ndi moyo zaka makumi atatu kudza ziwiri, nabala Serugi: ndipo Reu anakhala ndi moyo zaka mazana awiri kudza zisanu ndi ziwiri, atabala Serugi, nabala ana aamuna ndi aakazi. Ndipo Serugi anakhala ndi moyo zaka makumi atatu, nabala Nahori: ndipo Serugi anakhala ndi moyo zaka mazana awiri, atabala Nahori, nabala ana aamuna ndi aakazi. Ndipo Nahori anakhala ndi moyo zaka makumi awiri kudza zisanu ndi zinai, nabala Tera: ndipo Nahori anakhala ndi moyo zaka zana limodzi kudza khumi ndi zisanu ndi zinai, atabala Tera, nabala ana aamuna ndi aakazi. Ndipo Tera anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi awiri, nabala Abramu, ndi Nahori ndi Harani. Mibadwo ya Tera ndi iyi: Tera anabala Abramu, ndi Nahori, ndi Harani; ndipo Harani anabala Loti. Ndipo anafa Harani pamaso pa atate wake Tera m'dziko la kubadwa kwake, m'Uri wa kwa Akaldeya. Ndipo Abramu ndi Nahori, anadzitengera okha akazi; dzina lake la mkazi wa Abramu ndilo Sarai; ndi dzina lake la mkazi wa Nahori ndilo Milika, mwana wake wa Harani, atate wake wa Milika, ndi atate wake wa Isika. Koma Sarai anali wouma; analibe mwana. Ndipo Tera anatenga Abramu mwana wake wamwamuna, ndi Loti mwana wa Harani, mwana wake wamwamuna, ndi Sarai mpongozi wake, mkazi wa mwana wake Abramu; ndipo anatuluka pamodzi nao ku Uri wa kwa Akaldeya kuti amuke ku dziko la Kanani, ndipo anafika ku Harani, nakhala kumeneko. Masiku a Tera anali zaka mazana awiri kudza zisanu; ndipo anafa Tera m'Harani. Ndipo Yehova anati kwa Abramu, Tuluka iwe m'dziko lako, ndi kwa abale ako, ndi kunyumba ya atate wako, kunka ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe; ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso; ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi. Ndipo anamuka Abramu monga Yehova ananena kwa iye, ndipo Loti anamuka pamodzi naye: ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi awiri kudza zisanu, pamene anatuluka m'Harani. Ndipo Abramu anatenga Sarai mkazi wake, ndi Loti mwana wa mphwake, ndi chuma chao chimene anasonkhanitsa, ndi miyoyo imene anabala m'Harani; natuluka kunka ku dziko la Kanani, ndipo anadza ku dziko la Kanani. Ndipo Abramu anapitira m'dziko kufikira ku malo a Sekemu, kufikira ku mtengo wathundu wa ku More. Akanani anali m'dzikomo nthawi yomweyo. Ndipo Yehova anaonekera kwa Abramu nati, Ndidzapatsa mbeu yako dziko lino: pamenepo anammangira Yehova guwa la nsembe amene anamuonekera iye. Ndipo iye anachoka kumeneko kunka kuphiri la kum'mawa kwa Betele, namanga hema wake; Betele anali kumadzulo, ndi Ai anali kum'mawa: kumeneko ndipo anammangira Yehova guwa la nsembe, naitanira dzina la Yehova. Ndipo Abramu anayenda ulendo wake, nayendayenda kunka kumwera. Ndipo munali njala m'dzikomo, ndipo anatsikira Abramu ku Ejipito kukakhala kumeneko, chifukwa kuti njala inali yaikulu m'dziko m'menemo. Ndipo panali pamene anayandikira kulowa m'Ejipito, anati kwa Sarai mkazi wake, Taonani, ndidziwa kuti ndiwe mkazi wokongola maonekedwe ako; ndipo padzakhala pamene adzakuona iwe Aejipito, adzati, Uyu ndi mkazi wake: ndipo adzandipha ine, koma iwe adzakuleka ndi moyo. Uzikanenatu, kuti iwe ndiwe mlongo wanga: kuti chidzakhala chabwino ndi ine, chifukwa cha iwe, ndi kuti moyo wanga usungike ndi iwe. Ndipo panali pamene Abramu analowa m'Ejipito, Aejipito anaona kuti mkazi anali wokongola kwambiri. Ndipo akalonga ake a Farao anamuona iye, namyamikira iye kwa Farao; ndipo anamuka ndi mkazi kunyumba kwake kwa Farao. Ndipo anamchitira Abramu bwino chifukwa cha iyeyo; ndipo anali nazo nkhosa, ndi ng'ombe, ndi abulu, ndi akapolo, ndi adzakazi, ndi abulu akazi, ndi ngamira. Koma Yehova anavutitsa Farao ndi banja lake ndi nthenda zazikulu chifukwa cha Sarai mkazi wake wa Abramu. Ndipo Farao anaitana Abramu, nati, Nanga nchiyani ichi wandichitira ine? Chifukwa chanji sunandiuza ine kuti ndiye mkazi wako? Chifukwa chanji unati, Ndiye mlongo wanga? Kotero ndinamtenga iye akhale mkazi wanga; tsopano suyu mkazi wako; mtenge nuchoke. Ndipo Farao analamulira anthu ake za iye; ndipo anamperekeza iye m'njira ndi mkazi wake ndi zonse anali nazo. Ndipo anakwera Abramu kuchoka ku Ejipito, iye ndi mkazi wake, ndi zonse anali nazo, ndi Loti pamodzi naye, kunka ku dziko la kumwera. Ndipo Abramu anali wolemera ndithu ndi ng'ombe ndi siliva ndi golide. Ndipo anankabe ulendo wake kuchokera ku dziko la kumwera kunka ku Betele, kufikira kumalo kumene kunali hema wake poyamba paja pakati pa Betele ndi Ai; kumalo kwa guwa la nsembe analimanga iye kumeneko, poyamba paja; ndipo pamenepo Abramu anaitanira dzina la Yehova. Ndiponso Loti anayenda ndi Abramu anali ndi nkhosa ndi ng'ombe ndi mahema. Ndipo dziko silinathe kuwakwanira iwo, kuti akhale pamodzi: chifukwa kuti chuma chao chinali chambiri, ndipo sanathe kukhala pamodzi. Ndipo panali ndeu, abusa a Abramu kudana ndi abusa a Loti: Akanani ndi Aperizi ndipo analinkukhala nthawi yomweyo m'dzikomo. Ndipo Abramu anati kwa Loti, Tisachite ndeu, ine ndi iwe, abusa anga ndi abusa ako: chifukwa kuti ife ndife abale. Dziko lonse silili pamaso pako kodi? Ulekanetu ndi ine: ukanka iwe ku dzanja lamanzere, ine ndinka ku dzanja lamanja: ukanka iwe ku dzanja lamanja, ine ndinka ku dzanja lamanzere. Ndipo Loti anatukula maso ake nayang'ana chigwa chonse cha Yordani kuti chonsecho chinali ndi madzi ambiri, asanaononge Yehova Sodomu ndi Gomora, monga munda wa Yehova, monga dziko la Ejipito pakunka ku Zowari. Ndipo Loti anasankha chigwa chonse cha Yordani; ndipo Loti anachoka ulendo wake kunka kum'mawa: ndipo analekana wina ndi mnzake. Ndipo Abramu anakhala m'dziko la Kanani, ndipo Loti anakhala m'midzi ya m'chigwa, nasendeza hema wake kufikira ku Sodomu. Ndipo anthu a ku Sodomu anali oipa ndi ochimwa kwambiri pamaso pa Yehova. Ndipo Yehova anati kwa Abramu, atalekana naye Loti, Tukulatu maso ako, nuyang'anire kuyambira kumene uliko, kumpoto, ndi kumwera, ndi kum'mawa, ndi kumadzulo: chifukwa kuti dziko lonse limene ulinkuona, ndidzakupatsa iwe ndi mbeu yako nthawi yonse. Ndipo ndidzayesa mbeu yako monga fumbi lapansi: chotere kuti ngati munthu angathe kuwerenga fumbi lapansi, chomwechonso mbeu yako idzawerengedwa. Tauka, nuyendeyende m'dzikoli m'litali mwake ndi m'mimba mwake; chifukwa kuti ndidzakupatsa iwe limenelo. Ndipo Abramu anasuntha hema wake nafika nakhala pa mitengo yathundu ya pa Mamure, imene ili m'Hebroni, nammangira Yehova kumeneko guwa la nsembe. Ndipo panali masiku a Amurafere mfumu ya Sinara, ndi Ariyoki mfumu ya Elasara, ndi Kedorilaomere mfumu ya Elamu, ndi Tidala mfumu ya Goimu, iwo anathira nkhondo pa Bera mfumu ya Sodomu, ndi pa Birisa, mfumu ya Gomora, ndi pa Sinabe mfumu ya Adima, ndi pa Semebera mfumu ya Zeboimu, ndi pa mfumu ya Bela (kumeneko ndi ku Zowari). Onse amenewo anadziphatikana pa chigwa cha Sidimu (pamenepo ndi pa Nyanja ya Mchere). Zaka khumi ndi ziwiri iwo anamtumikira Kedorilaomere, chaka chakhumi ndi chitatu anapanduka. Chaka chakhumi ndi chinai ndipo anadza Kedorilaomere ndi mafumu amene anali naye, nawakantha Arefaimu m'Asiteroti-Karanaimu, ndi Azuzimu m'Hamu, ndi Aemimu m'Savekiriyataimu, ndi Ahori pa phiri lao Seiri kufikira ku Eliparani, kumene kuli m'mbali mwa chipululu. Ndipo anabwera nafika ku Enimisipati (kumeneko ndi ku Kadesi), nakantha dziko lonse la Aamaleke, ndiponso Aamori amene akhala m'Hazazoni-Tamara. Ndipo anatuluka mfumu ya Sodomu, ndi ya Gomora, ndi mfumu ya Adima, ndi mfumu ya Zeboimu, ndi mfumu ya Bela (kumeneko ndi ku Zowari) ndipo anawathira nkhondo m'chigwa cha Sidimu; ndi Kedorilaomere mfumu ya Elamu, ndi Tidala mfumu ya Goimu, ndi Amurafere mfumu ya Sinara, ndi Ariyoki mfumu ya Elasara; mafumu anai kugwirana ndi asanu. Chigwa cha Sidimu chinali ndi zitengetenge thoo; ndipo anathawa mafumu a ku Sodomu ndi Gomora nagwa m'menemo: amene anatsala anathawira kuphiri. Ndipo anatenga chuma chonse cha Sodomu ndi Gomora ndi zakudya zao zonse, namuka. Ndipo anagwira Loti mwana wa Abramu amene anakhala m'Sodomu, ndi chuma chake, namuka. Ndipo anadza wina amene anapulumuka namuuza Abramu Muhebri; ndipo iye analinkukhala pa mitengo yathundu ya pa Mamure Mwamori, mkulu wake wa Esikolo, ndi mkulu wake wa Anere; amenewo ndiwo opangana naye Abramu. Pamene anamva Abramu kuti mphwake anagwidwa, anatuluka natsogolera anyamata ake opangika, obadwa kunyumba kwake, mazana atatu kudza khumi ndi asanu ndi atatu, nawalondola kufikira ku Dani. Ndipo anadzigawanizira iwo usiku, iye ndi anyamata ake, nawakantha, nawapirikitsa kufikira ku Hoba, ndiko ku dzanja lamanzere la ku Damasiko. Ndipo anabwera nacho chuma chonse, nabwera naye Loti yemwe ndi chuma chake, ndi akazi ndi anthu omwe. Ndipo anatuluka mfumu ya Sodomu kukomana naye, atabwera anatha kuwakantha Kedorilaomere ndi mafumu amene anali naye, ku chigwa cha Save (ndiko ku chigwa cha mfumu), Ndipo Melkizedeki mfumu ya ku Salemu, anatuluka nao mkate ndi vinyo: iye ndiye wansembe wa Mulungu Wamkulukulu. Ndipo anamdalitsa iye, nati, Abramu adalitsike ndi Mulungu Wamkulukulu, mwini kumwamba ndi dziko lapansi; ayamikike Mulungu Wamkulukulu amene wapereka adani ako m'dzanja lako. Ndipo anampatsa iye limodzi la magawo khumi la zonse. Mfumu ya Sodomu ndipo inati kwa Abramu, Ndipatse ine anthu, nutenge chuma iwe wekha. Ndipo Abramu anati kwa mfumu ya Sodomu, Dzanja langa ndamtukulira Yehova, Mulungu Wamkulukulu, mwini kumwamba ndi dziko lapansi kuti sindidzatenga ngakhale thonje ngakhale chingwe cha nsapato, ngakhale kanthu kalikonse kako, kuti unganene, Ndamlemeza Abramu; koma chokhachi anadya anyamata, ndi gawo lao la anthu amene ananka pamodzi ndi ine, Anere, Esikolo, ndi Mamure, iwo atenge gawo lao. Zitapita izo, mau a Yehova anadza kwa Abramu m'masomphenya, kuti, Usaope, Abramu, Ine ndine chikopa chako ndi mphotho yako yaikulukulu. Ndipo Abramu anati, Ambuye Mulungu, mudzandipatsa ine chiyani popeza ndine wopanda mwana, ndi amene adzakhala mwini nyumba yanga ndiye Eliyezere wa ku Damasiko? Ndipo Abramu anati, Taonani, simunandipatse ine mbeu; ndipo, taonani, wobadwa m'nyumba mwanga adzalowa m'malo mwanga. Ndipo, taonani, mau a Yehova anadza kwa iye kuti, Uyu sadzakhala wakulowa m'malo mwako; koma iye amene adzatuluka m'chuuno mwako, ndiye adzakhala wakulowa m'malo mwako. Ndipo anamtulutsa iye kunja, nati, Tayang'anatu kumwamba, uwerenge nyenyezi, ngati ukhoza kuziwerenga zimenezo: ndipo anati kwa iye, Zoterezo zidzakhala mbeu zako. Ndipo anakhulupirira Yehova, ndipo kunayesedwa kwa iye chilungamo. Ndipo anati kwa iye, Ine ndine Yehova amene ndinatulutsa iwe m'Uri wa kwa Akaldeya, kuti ndikupatse iwe dziko limeneli likhale lakolako. Ndipo anati, Ambuye Mulungu, nanga ndidzadziwa bwanji kuti lidzakhala cholowa changa? Ndipo anati kwa iye, Kanditengere Ine ng'ombe yaikazi ya zaka zitatu, ndi mbuzi yaikazi ya zaka zitatu, ndi tonde wa zaka zitatu, ndi njiwa, ndi bunda. Ndipo anatenga iye zonse zimenezo, nazidula pakati, naika bandu popenyana ndi linzake: koma mbalame sanazidule. Pamene miimba inatsikira panyama, Abramu anaingitsa iyo. Ndipo linalinkulowa dzuwa, ndi tulo tatikulu tinamgwera Abramu: ndipo taonani, kuopsa kwa mdima waukulu kunamgwera iye. Ndipo anati kwa Abramu, Dziwitsa ndithu kuti mbeu zako zidzakhala alendo m'dziko la eni, nizidzatumikira iwo, ndipo iwo adzasautsa izo zaka mazana anai; ndiponso mtunduwo adzautumikira, Ine ndidzauweruza: ndiponso pambuyo pake adzatuluka ndi chuma chambiri. Ndipo iwe udzanka kwa makolo ako m'mtendere; nudzaikidwa ndi ukalamba wabwino. Koma iwo adzabweranso kuno mbadwo wachinai: pakuti mphulupulu za Aamori sizinakwaniridwe. Ndipo panali pamene litalowa dzuwa ndi kudza mdima, taonani, ng'anjo yofuka utsi ndi muuni wamoto wapita pakati pa mabanduwo. Tsiku lomwelo Yehova anapangana chipangano ndi Abramu, nati, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili, kuyambira pa mtsinje wa ku Ejipito kufikira pa mtsinje waukulu, mtsinje wa Yufurate: Akeni ndi Akenizi, Akadimoni, ndi Ahiti, ndi Aperizi, ndi Arefaimu, ndi Aamori, ndi Akanani, ndi Agirigasi, ndi Ayebusi. Ndipo Sarai mkazi wake wa Abramu sanambalire iye mwana; ndipo anali ndi mdzakazi, wa ku Ejipito, dzina lake Hagara. Ndipo Sarai anati kwa Abramu, Taonanitu, Yehova anandiletsa ine kuti ndisabale: lowanitu kwa mdzakazi wanga; kapena ndikalandire ndi iye ana. Ndipo Abramu anamvera mau a Sarai. Ndipo Sarai mkazi wake wa Abramu anatenga Hagara mdzakazi wake wa ku Ejipito, Abramu atakhala m'dziko la Kanani zaka khumi, nampereka iye kwa Abramu mwamuna wake, kuti akhale mkazi wake. Ndipo analowa kwa Hagara, ndipo iye anatenga pakati. Pamene anaona kuti anatenga pakati, anapeputsa wakuka wake m'maso mwake. Ndipo Sarai anati kwa Abramu, kusauka kwanga kukhale pa iwe: ndakupatsa iwe mdzakazi wanga pamtima pako; ndipo pakuona kuti anatenga pakati anandipeputsa ine m'maso mwake: Yehova aweruze pakati pa iwe ndi ine. Koma Abramu anati kwa Sarai, Taona, mdzakazi wako ali m'dzanja lako, umchitire iye chimene chikukomera m'maso mwako. Ndipo Sarai anamsautsa iye, ndipo anathawa kumaso kwake. Ndipo mthenga wa Yehova anampeza iye pa kasupe wa madzi m'chipululu, pa kasupe wa pa njira ya ku Suri. Ndipo anati, Hagara, mdzakazi wake wa Sarai, ufumira kuti? Unka kuti? Ndipo anati, Ndithawa ine kumaso kwake kwa wakuka wanga Sarai. Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Bwera kwa wakuka wako, udzichepetse wekha pamanja pake. Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Ndidzachulukitsa ndithu mbeu zako, kuti unyinji wao sudzawerengeka. Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Taona, uli ndi pakati, ndipo udzabala mwana wamwamuna; nudzamutcha dzina lake Ismaele; chifukwa Yehova anamva kusauka kwako. Ndipo iye adzakhala munthu wa m'thengo; ndipo dzanja lake lidzakhala lotsutsana ndi anthu onse, ndi manja a anthu onse adzakhala otsutsana naye: ndipo iye adzakhala pamaso pa abale ake onse. Ndipo anatcha dzina la Yehova amene ananena naye, Ndinu Mulungu wakundiona ine; pakuti anati, Kodi kunonso ndayang'ana pambuyo pake pa Iye amene wakundiona ine? Chifukwa chake chitsimecho chinatchedwa Beere-Lahai-Roi; taonani chili pakati pa Kadesi ndi Beredi. Ndipo Hagara anambalira Abramu mwana wamwamuna ndipo Abramu anatcha dzina la mwana wake amene anambalira iye Hagara, Ismaele. Ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi atatu kudza zisanu ndi chimodzi, pamene Hagara anambalira Abramu Ismaele. Pamene Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, Yehova anamuonekera Abramu nati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse; yenda iwe pamaso panga, nukhale wangwiro. Ndipo ndidzapangana pangano langa ndi Ine ndi iwe, ndipo ndidzachulukitsa iwe kwambiri. Ndipo Abramu anagwa nkhope pansi, ndipo Yehova ananena naye kuti, Koma Ine, taona, pangano langa lili ndi iwe, ndipo udzakhala iwe atate wa khamu la mitundu. Sudzatchedwanso dzina lako Abramu, koma dzina lako lidzakhala Abrahamu; chifukwa kuti ndakuyesa iwe atate wa khamu la mitundu. Ndipo ndikubalitsa iwe ndithu, ndipo ndidzakuyesa iwe mitundu, ndipo mafumu adzatuluka mwa iwe. Ndipo ndidzalimbitsa pangano langa ndi Ine ndi iwe pa mbeu zako za pambuyo pako m'mibadwo yao, kuti likhale pangano la nthawi zonse, kuti ndikhale Mulungu wako ndi wa mbeu zako za pambuyo pako. Ndipo ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako, dziko la maulendo anu, dziko lonse la Kanani likhale lako nthawi zonse: ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao. Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Koma iwe, uzikumbukira pangano langa, iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako m'mibadwo yao. Ili ndi pangano langa limene uzisunga pakati pa Ine ndi iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako: azidulidwa amuna onse a mwa inu. Muzidula khungu lanu; ndipo chidzakhala chizindikiro cha pangano pakati pa Ine ndi inu. A masiku asanu ndi atatu azidulidwa mwa inu, ana amuna onse m'mibadwo mwanu, amene abadwa m'nyumba ndi amene agulidwa ndi ndalama kwa alendo ali onse, wosakhala mwa mbeu zako. Azidulidwatu amene abadwa m'nyumba mwako ndi amene agulidwa ndi ndalama zako: ndipo pangano langa lidzakhala m'thupi mwako pangano losatha. Ndipo mwamuna wosadulidwa, wosadulidwa khungu lake, munthuyo amsadze mwa anthu a mtundu wake; waphwanya pangano langa. Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Koma Sarai mkazi wako, usam'tcha dzina lake Sarai, koma dzina lake ndi Sara. Ndipo ndidzamdalitsa iye, ndiponso ndidzakupatsa iwe mwana wamwamuna wobadwa mwa iye, inde, ndidzamdalitsa iye, ndipo adzakhala amake amitundu, mafumu a anthu adzatuluka mwa iye. Ndipo Abrahamu adagwa nkhope pansi, naseka, nati m'mtima mwake, Kodi mwana adzabadwa kwa iye amene ali wa zaka zana? Kodi Sara wa zaka makumi asanu ndi anai adzabala? Ndipo Abrahamu anati kwa Mulungu, Ha! Ismaele akhale ndi moyo pamaso panu! Ndipo Mulungu anati, Koma Sara mkazi wako adzakubalira iwe mwana wamwamuna; ndipo udzamutcha dzina lake Isaki; ndipo ndidzalimbikitsa naye pangano langa, kuti likhale pangano la nthawi zonse, la ku mbeu zake za pambuyo pake. Koma za Ismaele, ndamvera iwe: taona, ndamdalitsa iye, ndipo ndidzamchulukitsa iye ndithu; adzabala akalonga khumi ndi awiri, ndipo ndidzamuyesa iye mtundu waukulu. Koma pangano langa ndidzalimbikitsa ndi Isaki, amene Sara adzakubalira iwe nthawi yomwe yino chaka chamawa. Ndipo analeka kunena naye, ndipo Mulungu anakwera kuchokera kwa Abrahamu. Ndipo Abrahamu anatenga Ismaele mwana wake ndi onse amene anabadwa m'nyumba mwake, ndi onse amene anagulidwa ndi ndalama zake, amuna onse a mwa anthu a kunyumba kwake kwa Abrahamu, nadula khungu lao tsiku lomwelo, monga Mulungu ananena naye. Ndipo Abrahamu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, pamene anadulidwa m'khungu lake. Ndipo Ismaele mwana wake anali wa zaka khumi ndi zitatu pamene anadulidwa m'khungu lake. Tsiku lomwelo anadulidwa Abrahamu ndi Ismaele mwana wake. Ndipo amuna onse a m'nyumba mwake obadwa m'nyumba, ndi ogulidwa ndi ndalama kwa alendo, anadulidwa pamodzi naye. Ndipo Yehova anamuonekera iye pa mtengo yathundu ya ku Mamure, pamene anakhala pa khomo la hema wake pakutentha dzuwa. Ndipo anatukula maso ake, nayang'ana, taonani, anthu atatu anaima pandunji pake; pamene anaona iwo, anawathamangira kuchoka ku khomo la hema kukakomana nao, nawerama pansi, nati, Mbuyanga, ngatitu ndi ndikapeza ufulu pamaso panu, musapitiriretu pa kapolo wanu; nditengetu madzi pang'ono, ndikusambitseni mapazi anu, mupumule pansi pa mtengo; ndipo ndidzatenga chakudya pang'ono, nimutonthoze mitima yanu; mutatero mudzapitirira, chifukwa mwafika kwa kapolo wanu. Ndipo anati, Chita chomwecho monga momwe wanena. Ndipo Abrahamu analowa msanga m'hema wake kwa Sara, nati, Konza msanga miyeso itatu ya ufa wosalala, nuumbe, nupange mikate. Ndipo Abrahamu anafulumira kunka kuzoweta, natenga kamwana ka ng'ombe kofewa ndi kabwino, napatsa mnyamata, ndipo anafulumira kuphika. Ndipo anatenga mafuta amkaka, ndi mkaka, ndi kamwana ka ng'ombe kamene anaphika, naziika patsogolo pao; ndipo iye anaimirira iwo patsinde pa mtengo, ndipo anadya. Ndipo anati kwa iye, Ali kuti Sara mkazi wako? Ndipo anati, Taonani m'hemamo. Ndipo anati, Ndidzabwera kwa iwe ndithu pakufika nyengo yake; taonani Sara mkazi wako adzakhala ndi mwana wamwamuna. Ndipo Sara anamva pakhomo pa hema amene anali pambuyo pake. Koma Abrahamu ndi Sara anali okalamba, anapitirira masiku ao; ndipo kunaleka kwa Sara konga kumachita ndi akazi; ndipo Sara anaseka m'mtima mwake, nati, Kodi ndidzakhala ndi kukondwa ine nditakalamba, ndiponso mbuyanga ali wokalamba? Ndipo Yehova anati kwa Abrahamu, Bwanji anaseka Sara, kuti, Kodi ndidzabala ine ndithu, ine amene ndakalamba? Kodi chilipo chinthu chomkanika Yehova? Pa nthawi yoikidwa ndidzabwera kwa iwe, pakufika nyengo yake, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna. Koma Sara anakana, nati, Sindinasekai; chifukwa anaopa. Ndipo anati, Iai; koma unaseka. Ndipo anthuwo anauka kuchokera kumeneko nayang'ana ku Sodomu; ndipo Abrahamu ananka nao kuwaperekeza. Ndipo Yehova adati, Kodi ndidzabisira Abrahamu chimene ndichita? Pakuti Abrahamu adzakhala ndithu wamkulu ndi wamphamvu, ndipo mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsika mwa iye? Chifukwa ndamdziwa iye kuti alamulire ana ake ndi banja lake la pambuyo pake, kuti asunge njira ya Yehova, kuchita chilungamo ndi chiweruziro, kuti Yehova akamtengere Abrahamu chomwe anamnenera iye. Ndipo anati Yehova, Popeza kulira kwa Sodomu ndi Gomora kuli kwakukulu, ndipo popeza kuchimwa kwao kuli kulemera ndithu, ndidzatsikatu ndikaone ngati anachita monse monga kulira kwake kumene kunandifikira: ngati sanatero ndidzadziwa. Ndipo anthuwo anatembenuka nachoka kumeneko, napita kunka ku Sodomu. Koma Abrahamu anaimabe pamaso pa Yehova. Ndipo Abrahamu anayandikira nati, Kodi mudzaononga olungama pamodzi ndi oipa? Kapena alipo olungama makumi asanu m'kati mwa mudzi; kodi mudzaononga, simudzasiya malowo chifukwa cha olungama makumi asanu ali momwemo? Musamatero ai, kupha olungama pamodzi ndi oipa, kuta olungama akhale monga oipa; musamatero ai; kodi sadzachita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi? Ndipo anati Yehova, Ndikapeza m'Sodomu olungama makumi asanu m'kati mwa mudzi, ndidzasiya malo onse chifukwa cha iwo. Ndipo anayankha Abrahamu nati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye, ine ndine fumbi ndi phulusa: kapena akaperewera asanu pa olungama makumi asanuwo; kodi mudzaononga mudzi wonse chifukwa cha kuperewera asanu? Ndipo anati, Ndikapeza makumi anai ndi asanu sindidzauononga. Ndipo ananenanso kwa Iye nati, Kapena akapezedwa makumi anai m'menemo. Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha makumi anai. Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanenanso: kapena akapezedwa makumi atatu m'menemo? Ndipo anati, Ndikapeza makumi atatu m'menemo sindidzachita. Ndipo anati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye: kapena akapezedwa makumi awiri m'menemo. Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha makumi awiri. Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanena kamodzi aka kokha: kapena akapezedwa khumi m'menemo? Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha khumi. Ndipo Yehova anapita atatha kunena naye Abrahamu: ndipo Abrahamu anabwera kumalo kwake. Ndipo anadza ku Sodomu madzulo amithenga awiri; ndipo Loti anakhala pa chipata cha Sodomu, ndipo Loti anaona iwo, nauka kuti akakomane nao, ndipo anaweramitsa pansi nkhope yake. Ndipo anati, Taonanitu, Ambuye anga, tembenukanitu, kulowa m'nyumba mwa kapolo wanu, mugone usiku wonse, mutsuke mapazi anu, ndipo mudzalawira m'mawa kunka ulendo wanu. Ndipo anati, Iai; koma tigone m'khwalalamu usiku wonse. Ndipo anawaumiriza iwo ndithu: ndipo anapatukira kwa iye, nalowa m'nyumba mwake; ndipo anawakonzera iwo madyerero, naphika mikate yopanda chotupitsa, ndipo anadya. Koma asanagone, anthu a m'mudzimo anthu a Sodomu, anazinga nyumba, anyamata ndi okalamba, anthu onse a m'mbali zonse; ndipo anamuitana Loti, nati kwa iye, Ali kuti anthu amene anadza kwa iwe madzulo ano, utitulutsire iwo kuti tiwadziwe. Ndipo Loti anatulukira kwa iwo pakhomo, natseka chambuyo pakhomo pake. Ndipo anati, Abale anga, musachitetu koipa kotere. Taonanitu, ndili ndi ana akazi awiri, amene sanadziwe mwamuna; ndiwatulutsire iwo kwa inu, muchite nao chomwe chikomera inu; koma anthu awa musawachitire iwo kanthu; chifukwa kuti anadza iwo pansi pa mthunzi wa chindwi langa. Ndipo anati iwo, Baima; natinso, Uyu anadza kuno kukhala ngati mlendo, ndipo afuna kutilamulira; tsopano tidzakuchitira iwe koipa koposa iwo. Ndipo iwo anamkakamiza munthuyo Loti ndithu, nayandikira kuti aswe chitseko. Koma anthu aja anatulutsa dzanja lao, namlowetsa Loti momwe anali iwo m'nyumba, natseka pakhomo. Ndipo anachititsa khungu m'maso mwa anthu amene anali pakhomo pa nyumba, ang'ono ndi akulu, ndipo anavutika kufufuza pakhomo. Ndipo anthu aja anati kwa Loti, Kodi muli nao ena pano? Mkamwini, ndi ana ako amuna, ndi ana ako akazi, ndi onse ali nao m'mudzi muno, utuluke nao m'malo muno: popeza ife tidzaononga malo ano, chifukwa kulira kwao kwakula pamaso pa Yehova, ndipo Yehova anatitumiza ife kuti tiuononge. Ndipo anatuluka Loti nanena nao akamwini ake amene anakwata ana ake akazi, nati, Taukani, tulukani m'malo muno; popeza Yehova adzaononga mudziwu; koma akamwini ake anamyesa wongoseka. Pamene kunacha, amithengawo anafulumiza Loti, nati, Uka, tenga mkazi wako, ndi ana ako akazi awiri amene ali kunowa, kuti munganyeke m'mphulupulu ya mudzi. Koma anachedwa; ndipo anthuwo anamgwira dzanja lake, ndi dzanja la mkazi wake ndi dzanja la ana ake akazi awiri; chifukwa cha kumchitira chifundo Yehova; ndipo anamtulutsa iye, namuika kunja kwa mudzi. Ndipo panali pamene anawatulutsa iwo kunja, anati, Tapulumuka ndi moyo wako; usacheuke, usakhale pachigwa paliponse; thawira kuphiri, kuti unganyeke. Ndipo Loti anati kwa iwo, Iaitu, mfumu; taonanitu, kapolo wanu anapeza ufulu pamaso panu, ndipo munakuza chifundo chanu, chimene munandichitira ine, pakupulumutsa moyo wanga; ine sindikhoza kuthawira kuphiri kuti chingandipeze ine choipacho ndingafe; taonanitu, mudzi uwu uli pafupi pothawirapo, ndipo uli waung'ono; ndithawiretu kumeneko, suli waung'ono nanga? Ndipo ndidzakhala ndi moyo. Ndipo anati kwa iye, Taona, ndikuvomereza iwe pamenepanso kuti sindidzaononga mudzi uwu umene wandiuza. Fulumira, thawira kumeneko; pakuti sindithai kuchita kanthu usadafike kumeneko. Chifukwa chake anatcha dzina la mudziwo Zowari. Ndipo dzuwa lidakwera pa dziko pamene Loti anafika ku Zowari. Ndipo Yehova anavumbitsa pa Sodomu ndi pa Gomora miyala ya sulufure ndi moto kutuluka kwa Mulungu kumwamba; ndipo anaononga midziyo, ndi chigwa chonse, ndi onse akukhala m'midzimo, ndi zimene zimera panthaka. Koma mkazi wake anacheuka ali pambuyo pake pa Loti, nasanduka mwala wamchere. Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa kunka kumalo kumene anaima pamaso pa Yehova: ndipo anayang'anira ku Sodomu ndi ku Gomora ndi ku dziko lonse la chigwa, ndipo anapenya, taonanitu, utsi wa dzikolo unakwera, monga utsi wa ng'anjo. Ndipo panali pamene Mulungu anaononga midzi ya m'chigwa, Mulungu anakumbukira Abrahamu, natulutsa Loti pakati pa chionongeko, pamene anaononga midzi m'mene anakhalamo Loti. Ndipo Loti anabwera kutuluka m'Zowari nakhala m'phiri ndi ana akazi awiri pamodzi naye: chifukwa anaopa kukhala m'Zowari, ndipo anakhala m'phanga, iye ndi ana ake akazi. Woyamba ndipo anati kwa wamng'ono, Atate wathu akalamba, ndipo palibe pa dziko lapansi mwamuna amene adzalowa kwa ife monga amachita pa dziko lonse lapansi: tiyeni, timwetse atate vinyo, tidzagona naye, kuti tisunge mbeu za atate wathu. Ndipo anamwetsa atate wao vinyo usiku womwewo; woyamba ndipo analowa nagona naye atate wake; ndipo sanadziwe pomwe anagona ndi pomwe anauka. Ndipo panali m'mamawa, woyamba anati kwa wamng'ono, Taona, ndinagona ine ndi atate wanga usiku walero: timwetsenso iye usikunso: udzalowe nugone naye kuti tisunge mbeu za atate wathu. Ndipo anamwetsa vinyo atate wao usiku womwenso; wamng'ono ndipo anauka nagona naye; ndipo iye sanadziwe pomwe anagona ndi pomwe anauka. Ndipo ana akazi awiri a Loti anali ndi pakati pa atate wao. Woyamba ndipo anabala mwana wamwamuna, namtcha dzina lake. Mowabu; yemweyo ndi atate wa Amowabu kufikira lero. Wamng'ono ndipo anabala mwana wamwamuna, namtcha dzina lake Benami; yemweyo ndi atate wa Aamoni kufikira lero. Abrahamu ndipo anachoka kumeneko kunka ku dziko la kumwera, ndipo anakhala pakati pa Kadesi ndi Suri, ndipo anakhala ngati mlendo m'Gerari. Ndipo Abrahamu anati za Sara mkazi wake, Iye ndiye mlongo wanga: ndipo Abimeleki mfumu ya Gerari anatumiza namtenga Sara Koma Mulungu anadza kwa Abimeleki m'kulota kwa usiku, nati kwa iye, Taona, wakufa iwe, chifukwa cha mkazi amene wamtenga: pakuti iye ndiye mkazi wa mwini. Koma Abimeleki sanayandikire naye; ndipo anati, Ambuye, kodi mudzaphanso mtundu wolungama? Kodi iye sanati kwa ine, Ndiye mlongo wanga: ndipo mkazi iye yekha anati, Iye ndiye mlongo wanga: ndi mtima wanga wangwiro ndi manja anga osachimwa ndachita ine ichi. Ndipo Mulungu anati kwa iye m'kulota, Inde ndidziwa Ine, kuti wachita icho ndi mtima wangwiro, ndipo Inenso ndinakuletsa iwe kuti usandichimwire ine: chifukwa chake sindinakuloleza iwe kuti umkhudze mkaziyo. Tsopano, umbwezere munthuyo mkazi wake; chifukwa iye ndiye mneneri, ndipo adzakupempherera iwe, ndipo udzakhala ndi moyo: koma ukaleka kumbwezera, udziwe kuti udzafa ndithu, iwe ndi onse amene uli nao. Ndipo Abimeleki analawira m'mamawa, naitana anyamata ake onse, nanena zonse zimenezo m'makutu mwao, ndipo anthu anaopa kwambiri Ndipo Abimeleki anaitana Abrahamu, nati kwa iye, Watichitira ife chiyani iwe? Ndakuchimwiranji iwe kuti waufikitsa pa ine ndi pa ufumu wanga uchimo waukulu? Wandichitira ine zosayenera kuzichita. Ndipo Abimeleki anati kwa Abrahamu, Unaona chiyani iwe kuti wachita ichi? Ndipo Abrahamu anati, Chifukwa ndinati, Pompano palibe ndithu kumuopa Mulungu, ndipo adzandipha ine chifukwa cha mkazi wanga. Koma ndiye mlongo wanga ndithu, mwana wa atate wanga, koma si mwana wa amai wanga: ndipo anakhala ndi ine mkazi wanga. Ndipo panali pamene Mulungu anandiyendetsa ine kunyumba kwa atate wanga, ndinati kwa mkaziyo, Ichi ndicho chokoma mtima udzandichitire ine, konse kumene tidzafika ife, uzinena za ine, Iye ndiye mlongo wanga. Ndipo Abimeleki anatenga nkhosa ndi ng'ombe ndi akapolo ndi adzakazi nampatsa Abrahamu, nambwezera iye Sara mkazi wake. Ndipo Abimeleki anati, Taona dziko langa lili pamaso pako; kumene kuli kwabwino pamaso pako takhala kumeneko. Kwa Sara ndipo anati, Taona, ndapatsa mlongo wako ndalama zasiliva mazana khumi; taona, izo ndizo zoyeretsa maso za kwa onse amene ali ndi iwe: ndi pamaso pa onse ukhale wolungama. Ndipo Abrahamu anapemphera Mulungu, ndipo Mulungu anachiritsa Abimeleki, ndi mkazi wake, ndi adzakazi ake; ndipo anabala ana. Pakuti Yehova anatseketsa mimba yonse ya a m'nyumba ya Abimeleki, chifukwa cha Sara mkazi wake wa Abrahamu. Ndipo Yehova anayang'anira Sara monga momwe anati, ndipo Yehova anamchitira iye monga ananena. Ndipo Sara anatenga pakati, nambalira Abrahamu m'ukalamba wake mwana wamwamuna, nthawi yomweyo Mulungu anamuuza iye. Ndipo Abrahamu anamutcha dzina lake la mwana wake wamwamuna amene anabala iye, amene anambalira iye Sara, Isaki. Ndipo Abrahamu anamdula mwana wake wamwamuna Isaki pamene anali wa masiku ake asanu ndi atatu, monga Mulungu anamlamulira iye. Ndipo Abrahamu anali wa zaka zana limodzi pamene anambadwira iye Isaki mwana wake. Ndipo Sara anati, Mulungu anandisekeretsa ine; onse akumva adzasekera pamodzi ndi ine. Ndipo anati, Akadatero ndani kwa Abrahamu kuti Sara adzayamwitsa ana? Pakuti ndambalira iye mwana wamwamuna m'ukalamba wake. Ndipo anakula mwanayo naletsedwa kuyamwa: ndipo Abrahamu anakonza madyerero akulu tsiku lomwe analetsedwa Isaki kuyamwa. Ndipo Sara anaona mwana wake wamwamuna wa Hagara Mwejipito, amene anambalira Abrahamu, alinkuseka. Chifukwa chake anati kwa Abrahamu, Chotsa mdzakazi uyo, ndi mwana wake wamwamuna; chifukwa mwana wa mdzakazi uyo sadzalowa m'nyumba pamodzi naye mwana wanga Isaki. Ndipo mauwo anaipira Abrahamu chifukwa cha mwana wake. Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Usaipidwe nao, chifukwa cha mnyamatayo, ndi chifukwa cha mdzakazi wako; momwe monse akunenera iwe Sara umvere iwe mau ake; chifukwa kuti mwa Isaki zidzaitanidwa mbeu zako. Ndipo mwana wamwamuna wa mdzakazi uyo ndidzayesa mtundu, chifukwa iye ndiye mbeu yako. Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa, natenga mkate ndi mchenje wa madzi, nampatsa Hagara, naika paphewa pake, ndi mwana, namchotsa iye: ndipo iye anamuka, nasocherera m'chipululu cha Beereseba. Ndipo anatha madzi a m'mchenje ndipo anaika mwana pansi pa chitsamba. Ndipo ananka nakhala pansi popenyana naye patali, monga pakugwa muvi: chifukwa anati, Ndisaone kufa kwa mwana. Ndipo anakhala popenyana naye, nakweza mau ake nalira. Ndipo Mulungu anamva mau a mnyamatayo, ndi mthenga wa Mulungu anamuitana Hagara, ndi mau odzera kumwamba, nati kwa iye, Watani Hagara? Usaope; chifukwa Mulungu anamva mau a mnyamata kumene ali. Tauka, nuukitse mnyamatayo, ndi kumgwira m'dzanja lako; chifukwa ndidzamuyesa iye mtundu waukulu. Ndipo Mulungu anamtsegula m'maso mwake, ndipo anaona chitsime cha madzi; namuka nadzaza mchenje ndi madzi, nampatsa mnyamata kuti amwe. Ndipo Mulungu anakhala ndi mnyamata, ndipo anakula iye; nakhala m'chipululu, nakhala wauta. Ndipo anakhala m'chipululu cha Parani; ndipo amake anamtengera iye mkazi wa ku dziko la Ejipito. Ndipo panali nthawi yomweyo, Abimeleki ndi Fikolo kazembe wa nkhondo yake anati kwa Abrahamu, kuti, Mulungu ali pamodzi ndi iwe m'zonse uzichita iwe; tsopano iwe undilumbirire ine pano pa Mulungu kuti sudzandinyenga ine, kapena mwana wanga, kapena mdzukulu wanga: koma monga ufulu ndakuchitira iwe udzandichitire ine, ndi dziko lomwe wakhalamo, ngati mlendo. Ndipo Abrahamu anati, Ine ndidzalumbira. Ndipo Abrahamu anamdzudzula Abimeleki chifukwa cha chitsime cha madzi, anyamata ake a Abimeleki anachilanda. Ndipo anati Abimeleki, Sindinadziwe amene anachita icho; ndipo iwe sunandiuze ine, ndiponso sindinamve koma lero lino. Ndipo Abrahamu anatenga nkhosa ndi ng'ombe, nampatsa Abimeleki, ndipo anapangana pangano onse awiriwo. Ndipo Abrahamu anapatula anaankhosa akazi asanu ndi awiri pa okha. Ndipo Abimeleki anati kwa Abrahamu, Nanga anaankhosa akazi asanu ndi awiri amene wapatula pa okha? Ndipo anati, Anaankhosa akazi asanu ndi awiriwa uwalandire pa dzanja langa, kuti akhale mboni zanga, kuti ndakumba ine chitsime chimenechi. Chifukwa chake anatcha malowo Beereseba: chifukwa pamenepo analumbira onse awiri. Ndipo anapangana pangano pa Beereseba: ndipo anauka Abimeleki ndi Fikolo kazembe wa nkhondo yake, nabwera kunka ku dziko la Afilisti. Ndipo Abrahamu anaoka mtengo wa bwemba pa Beereseba, naitanira pamenepo dzina la Yehova, Mulungu wa nthawi zonse. Ndipo Abrahamu anakhala ngati mlendo masiku ambiri m'dziko la Afilisti. Ndipo panali zitapita zimenezo, Mulungu anamuyesa Abrahamu nati kwa iye, Abrahamu; ndipo anati, Ndine pano. Ndipo anati, Tengatu mwana wako, wamwamuna wayekhayo, Isaki, amene ukondana naye, numuke ku dziko la Moriya; numpereke iye kumeneko nsembe yopsereza pa limodzi la mapiri lomwe ndidzakuuza iwe. Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa namanga bulu wake, natengako anyamata ake awiri pamodzi naye, ndi Isaki mwana wake, nawaza nkhuni za nsembe yopsereza, nauka, nanka kumalo komwe Mulungu anamuuza iye. Tsiku lachitatu Abrahamu anatukula maso ake naona malowo patali. Ndipo Abrahamu anati kwa anyamata ake, Khalani kuno ndi bulu, ine ndi mwanayu tinka uko, ndipo tikapemphera ndi kubweranso kwa inu. Ndipo Abrahamu anatenga nkhuni za nsembe yopsereza, nazisenzetsa Isaki mwana wake; natenga moto m'dzanja lake ndi mpeni; nayenda pamodzi onse awiri. Ndipo Isaki ananena ndi Abrahamu atate wake, nati, Atate wanga; ndipo iye anati, Ndine pano, mwana wanga. Ndipo anati, Taonani moto ndi nkhuni; koma mwanawankhosa wa nsembe yopsereza ali kuti? Ndipo Abrahamu anati, Mwana wanga, Mulungu adzadzifunira yekha mwanawankhosa wa nsembe yopsereza; nayenda pamodzi onse awiri. Ndipo anafika kumalo komwe Mulungu anamuuza iye; ndipo Abrahamu anamanga guwa la nsembe nakonza nkhuni, namanga Isaki mwana wake, namuika iye pa guwa la nsembe pamwamba pa nkhuni. Ndipo Abrahamu anatambasula dzanja lake, natenga mpeni kuti amuphe mwana wake. Koma mthenga wa Yehova anamuitana iye ndi mau odzera kumwamba, nati, Abrahamu, Abrahamu; ndi iye anati, Ndine pano. Ndipo mthenga anati, Usaike dzanja lako pa mwana, usamchitire iye kanthu; chifukwa tsopano ndidziwa kuti iwe umuopa Mulungu wako, pakuti sunandikanize ine mwana wako, mwana wako wayekha. Ndipo Abrahamu anatukula maso ake nayang'ana taonani, pambuyo pake nkhosa yamphongo yogwiridwa ndi nyanga zake m'chiyangoyangomo; ndipo ananka Abrahamu nakatenga nkhosa yamphongoyo, naipereka nsembe yopsereza m'malo mwa mwana wake. Ndipo Abrahamu anatcha dzina lake la malowo Yehova-Yire: monga ati lero lomwe, M'phiri la Yehova chidzaoneka. Ndipo mthenga wa Yehova anamuitana Abrahamu ndi mau odzera kumwamba kachiwiri, nati, Pa Ine ndekha ndalumbira, ati Yehova, popeza wachita ichi, sunandikaniza mwana wako, mwana wako yekha, kudalitsa ndidzakudalitsa iwe, kuchulukitsa ndidzachulukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, monga mchenga wa m'mphepete mwa nyanja; ndipo mbeu zako zidzagonjetsa chipata cha adani ao; m'mbeu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa: chifukwa wamvera mau anga. Ndipo Abrahamu anabwera kwa anyamata ake, ndipo anauka nayenda pamodzi kumuka ku Beereseba; ndipo anakhala Abrahamu pa Beereseba. Ndipo panali zitapita izi, anauza Abrahamu kuti, Taonani, Milika iyenso anambalira Nahori mphwako ana; Uzi woyamba ndi Buzi mphwake, ndi Kemuwele atate wake wa Aramu; ndi Kesedi, ndi Hazo, ndi Pilidasi ndi Yidilafi, ndi Betuele. Ndimo Betuele anabala Rebeka: amenewa asanu ndi atatu Milika anambalira Nahori mphwake wa Abrahamu. Ndipo mkazi wake wamng'ono, dzina lake Reuma, iyenso anabala Teba, ndi Gahamu, ndi Tahasi, ndi Maaka. Ndipo Sara anali wa zaka zana limodzi kudza makumi awiri ndi zisanu ndi ziwiri: ndizo zaka za moyo wa Sara. Ndipo Sara anafa m'Kiriyati-Ariba (ndiwo Hebroni), m'dziko la Kanani; ndipo Abrahamu anadza ku maliro a Sara, kuti amlire. Ndipo Abrahamu anauka pa wakufa wake, nanena kwa ana a Hiti, nati, Ine ndine mlendo wakukhala ndi inu: mundipatse ndikhale ndi manda pamodzi ndi inu, kuti ndiike wakufa wanga ndisamthirenso maso. Ndipo ana a Hiti anayankha Abrahamu nati kwa iye, Mutimvere ife mfumu, ndinu kalonga wamkulu pakati pa ife; muike wakufa wanu m'manda mwathu mosankhika: palibe munthu yense wa ife adzakaniza manda ake, kuti muike wakufa wanu. Ndipo anauka Abrahamu naweramira anthu a m'dzikomo, ana a Hiti. Ndipo ananena nao, kuti, Ngati mukandivomereza kuti ndiike wakufa wanga ndisamthirenso maso, mundimvere ine, mundinenere ine kwa Efuroni mwana wake wa Zohari, kuti andipatse ine phanga la Makipela, limene lili pansonga pa munda wake; pa mtengo wake wonse andipatse pakati pa inu, ndikhale nao manda. Ndipo Efuroni anakhala pakati pa ana a Hiti: ndipo Efuroni Muhiti anayankha Abrahamu alinkumva ana a Hiti, onse amene analowa pa chipata cha mudzi wake, kuti, Iai, mfumu, mundimvere ine; munda ndikupatsani inu, ndi phanga lili m'menemo ndikupatsani inu, pamaso pa ana a anthu anga ndikupatsani inu; ikani wakufa wanu. Ndipo Abrahamu anawerama pamaso pa anthu a m'dzikomo. Ndipo ananena kwa Efuroni alinkumva anthu a m'dzikomo, kuti, Koma ngati ufuna, undimveretu ine: ndidzakupatsa iwe mtengo wake wa munda; uulandire kwa ine, ndipo ndidzaika wakufa wanga m'menemo. Ndipo Efuroni anamyankha Abrahamu, nati kwa iye, Mfumu, mundimvere ine; kadziko ka mtengo wake wa masekeli a siliva mazana anai, ndiko chiyani pakati pa ine ndi inu? Ikani wakufa wanu. Ndipo Abrahamu anamvera Efuroni, ndipo Abrahamu anamuyesera Efuroni ndalama zimene ananena alinkumva ana a Hiti, masekeli a siliva mazana anai, ndalama zomwezo agulana nazo malonda. Ndipo munda wa Efuroni umene unali m'Makipela, umene unali patsogolo pa Mamure, munda ndi phanga lili momwemo, ndi mitengo yonse inali m'mundamo, yokhala m'malire monse mozungulira momwemo, inalimbitsidwa kwa Abrahamu ikhale yake, pamaso pa ana a Hiti, pa onse amene analowa pa chipata cha mudzi wake. Zitatha izi Abrahamu anaika Sara mkazi wake m'phanga la munda wa Makipela patsogolo pa Mamure (ndiwo Hebroni), m'dziko la Kanani. Ndipo ana a Hiti analimbitsira Abrahamu munda, ndi phanga lili m'menemo, likhale lake lamanda. Ndipo Abrahamu anali wokalamba, nagonera zaka zambiri; ndipo Yehova anadalitsa Abrahamu m'zinthu zonse. Ndipo Abrahamu anati kwa mnyamata wake wamkulu wa pa nyumba yake, amene analamulira pa zonse anali nazo, Taikatu dzanja lako pansi pa ntchafu yanga: ndipo ndidzakulumbiritsa iwe pa Yehova, Mulungu wa Kumwamba, ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti usadzamtengere mwana wanga mkazi wa kwa ana akazi a Akananiwo, amene ndikhala pakati pao. Koma udzanke ku dziko langa, kwa abale anga, ndi kumtengera mwana wanga Isaki mkazi. Ndipo anati kwa iye mnyamatayo, Kapena sadzafuna mkaziyo kunditsata ine ku dziko lino: kodi ndikambwezerenso mwana wanu ku dziko komwe mwachokera inu? Ndipo Abrahamu anati kwa iye, Chenjera iwe, usambwezerenso mwana wanga kumeneko. Yehova Mulungu wa Kumwamba, amene ananditenga ine kunyumba ya atate wanga, ku dziko la abale anga, amene ananena ndi ine, amene analumbirira ine kuti, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili; Iye adzatumiza mthenga wake akutsogolere, ndipo udzamtengere mwana wanga mkazi kumeneko. Ndipo ngati sadzafuna mkaziyo kukutsata iwe, udzakhala wosachimwa pa chilumbiro changachi: koma mwana wanga usambwezerenso kumeneko. Ndipo mnyamatayo anaika dzanja lake pansi pa ntchafu yake ya Abrahamu Mbuye wake, namlumbirira iye za chinthucho. Ndipo mnyamatayo anatenga ngamira khumi za mbuyake, namuka: chifukwa kuti chuma chonse cha mbuyake chinali m'dzanja lake: ndipo anachoka namuka ku Mesopotamiya, kumudzi wa Nahori. Ndipo anagwaditsa ngamira zake kunja kwa mudzi, ku chitsime cha madzi nthawi yamadzulo, nthawi yotuluka akazi kudzatunga madzi. Ndipo anati, Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu mundiyendetse ine bwino lero lino, mumchitire ufulu mbuyanga Abrahamu. Taonani, ine ndiima pa chitsime cha madzi; ndipo ana akazi a m'mudzi atuluka kudzatunga madzi; ndipo pakhale kuti namwali amene ndidzati kwa iye, Tulatu mtsuko wako, ndimwe; ndipo iye adzati, Imwa, ndipo ndidzamwetsanso ngamira zako; yemweyo akhale mkazi wosankhira mnyamata wanu Isaki; ndipo chotero ndidzadziwa kuti mwamchitira mbuyanga ufulu. Ndipo panali, asanathe kunena, taonani, anatuluka Rebeka, amene anambala Betuele, mwana wamwamuna wa Milika, mkazi wa Nahori mphwake wa Abrahamu, ndi mtsuko wake paphewa pake. Ndipo namwaliyo anali wokongola kwambiri m'maonekedwe ake, ndiye namwali wosamdziwa mwamuna, ndipo anatsikira kukasupe, nadzaza mtsuko wake, nakwera. Ndipo mnyamatayo anamthamangira kukomana naye, nati, Ndimwetu madzi pang'ono a m'mtsuko mwako. Ndipo anati, Imwa mbuyanga; nafulumira nayangata mtsuko m'manja mwake namwetsa iye. Atatha kumwetsa iye, anati, Ndidzatungiranso ngamira zako, mpaka zitamwa zonse. Ndipo anafulumira nathira madzi a m'mtsuko wake m'chomwera, nathamangiranso kuchitsime kukatunga, nazitungira ngamira zake zonse. Munthuyo ndipo anamyang'anira iye, nakhala chete, kuti adziwe ngati Yehova anamuyendetsa bwino kapena iai. Ndipo panali zitatha kumwa ngamira, munthuyo anatenga mphete yagolide ya kulemera kwake sekeli latheka, ndi zingwinjiri ziwiri za m'manja ake, kulemera kwake masekeli khumi a golide. Ndipo anati, Ndiwe mwana wa yani? Undiuzetu. Kodi kunyumba ya atate wako kuli malo akuti tigoneko ife? Ndipo mkaziyo anati kwa iye, Ine ndine mwana wa Betuele mwana wamwamuna wa Milika, amene anambalira Nahori. Natinso kwa iye, Tili nao udzu ndi zakudya zambiri ndi malo ogona. Munthuyo ndipo anawerama mutu namyamika Yehova. Ndipo anati, Ayamikike Yehova Mulungu wa Ambuyanga Abrahamu amene sanasiye mbuyanga wopanda chifundo chake ndi zoona zake: koma ine Yehova wanditsogolera m'njira ya kunyumba ya abale ake a mbuyanga. Namwaliyo ndipo anathamanga nawauza zimenezo kunyumba ya amake. Ndipo Rebeka anali ndi mlongo wake dzina lake Labani; ndipo Labani anathamangira munthuyo kunja ku kasupe. Ndipo panali, pamene anaona mphete ndi zingwinjiri pa manja a mlongo wake, pamene anamva mau a Rebeka mlongo wake, akuti, Chotero ananena ndi ine munthuyo; Labani anafika pa munthuyo; taonani, anaimirira pa ngamira pakasupe. Ndipo anati, Talowa iwe, wodalitsidwa ndi Yehova; uimiriranji kunjako? Chifukwa kuti ndakonzeratu nyumba, ndi malo a ngamira. Munthuyo ndipo analowa m'nyumba, namasula ngamira, napatsa ngamira udzu ndi chakudya, ndi madzi akusamba mapazi ake ndi mapazi a iwo amene anali naye. Ndipo anaika chakudya pamaso pake: koma anati, Sindidzadya ndisananene chimene ndadzera. Ndipo anati, Nenatu. Ndipo anati, Ine ndine mnyamata wa Abrahamu. Yehova wamdalitsa mbuyanga kwambiri; ndipo analemera kwakulukulu; ndipo anampatsa iye nkhosa ndi ng'ombe, ndi siliva ndi golide, ndi akapolo ndi adzakazi, ndi ngamira ndi abulu. Ndipo Sara mkazi wake wa mbuyanga anambalira mbuyanga mwana wamwamuna, mkaziyo anali wokalamba; ndipo anampatsa mwanayo zonse ali nazo. Ndipo mbuyanga anandilumbiritsa ine kuti, Usamtengere mwana wanga mkazi wa ana akazi a Kanani, m'dziko mwao m'mene ndikhala ine; koma udzanke kunyumba ya atate wanga, kwa abale anga, ndi kumtengera mwana wanga mkazi. Ndipo ndinati kwa mbuyanga, Kapena mkazi sadzanditsata ine. Ndipo anati kwa ine, Yehova, amene ndiyenda ine pamaso pake, adzatumiza mthenga wake pamodzi ndi iwe, nadzakuyendetsa bwino m'njira yako; ndipo ukamtengere mwana wanga mkazi wa mwa abale anga ndi kunyumba ya atate wanga; ukatero udzakhala wosachimwa pa malumbiro ako, pofika iwe kwa abale anga; ndipo ngati sadzakupatsa iwe, udzakhala wosachimwa pa malumbiro ako. Ndipo ndinafika lero kukasupe, ndipo ndinati, Yehova Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, ngati mundiyendetsatu bwino njira yanga m'mene ndinkamo ine; taonani, ine ndiima pa kasupe wa madzi, ndipo pakhale, kuti namwali amene atuluka kudzatunga madzi ndimwe pang'ono m'mtsuko mwako; ndipo iye akati kwa ine, Imwatu iwe, ndiponso ndidzatungira ngamira zako; yemweyo akhale mkazi amene Yehova wamsankhira mwana wa mbuyanga. Ndisanathe kunena m'mtima mwanga, taonani, Rebeka anatuluka ndi mtsuko wake pa phewa lake, natsikira ku kasupe, natunga: ndipo ndinati kwa iye, Ndimwetu. Ndipo iye anafulumira, natsitsa mtsuko pa phewa lake, nati, Imwatu, ndipo ndidzamwetsanso ngamira zako: ndipo ndinamwa, ndipo anamwetsa ngamira. Ndipo ndinamfunsa iye kuti, Ndiwe mwana wa yani kodi? Ndipo anati, Ndine mwana wa Betuele, mwana wa Nahori amene anambalira iye Milika: ndipo ndinaika mphete pambuyo pake ndi zingwinjiri pa manja ake. Ndipo ndinawerama mutu wanga ndi kulambira Yehova, ndi kumyamikira Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, amene ananditsogolera ine m'njira yakuona, kuti ndikamtengere mwana wamwamuna wake mwana wa mkazi wa mphwake wa mbuyanga. Tsopano, ngati mudzamchitira mbuyanga zaufulu ndi zoonadi, mundiuze, ngati iai, mundiuze; kuti ndipatukire ku dzanja lamanja kapena ku dzanja lamanzere. Ndipo anayankha Labani ndi Betuele, nati, Chatuluka kwa Yehova chinthu ichi; sitingathe kunena ndi iwe choipa kapena chabwino. Taonani, Rebeka ali pamaso pako, mtenge ndi kumuka, akhale mkazi wa mwana wa mbuyako, monga wanena Yehova. Ndipo panali pamene anamva mauwo mnyamata wa Abrahamu, anamgwadira Yehova pansi. Ndipo mnyamatayo anatulutsa zokometsera zasiliva ndi zagolide, ndi zovala, nampatsa Rebeka: ndipo anapatsa za mtengo wapatali kwa mlongo wake ndi amake. Ndipo anadya namwa iye ndi anthu amene anali pamodzi naye, nagonapo usiku: ndipo anauka m'mamawa, ndipo iye anati, Mundilole ine ndinke kwa mbuyanga. Ndipo mlongo wake ndi amake anati, Namwali akhale ndi ife masiku akuwerengeka, afikire khumi; patsogolo pake iye adzamuka. Ndipo iye anati kwa iwo, Musandichedwetse ine, pakuti Yehova wandiyendetsa bwino m'njira yanga: mundilole ine ndinke kwa mbuyanga. Ndipo anati iwo, Tidzamuitana namwaliyo, tidzamfunsa pakamwa pake. Ndipo anamuitana Rebeka nati kwa iye, Kodi udzanka pamodzi ndi munthuyo? Ndipo anati, Ndidzanka. Ndipo anamlola Rebeka mlongo wao ndi mlezi wake, amuke pamodzi ndi mnyamata wake wa Abrahamu, ndi anthu ake. Ndipo anamdalitsa Rebeka, nati kwa iye, Mlongo wathu ndiwe, iwe ukhale amai wa anthu zikwizikwi, mbeu zako zigonjetse chipata cha iwo akudana nao. Ndipo adauka Rebeka ndi anamwali ake, nakwera pa ngamira natsata munthuyo: mnyamatayo ndipo anamtenga Rebeka namuka. Ndipo Isaki anadzera njira ya Beere-Lahai-Roi; chifukwa kuti anakhala iye m'dziko la kumwera. Ndipo Isaki anatuluka kulingalira m'munda madzulo; ndipo anatukula maso ake, nayang'ana, taona, ngamira zinalinkudza. Ndipo Rebeka anatukula maso ake, ndipo pamene anaona Isaki anatsika pa ngamira. Ndipo anati kwa mnyamata, Munthuyo ndani amene ayenda m'munda kukomana ndi ife? Mnyamatayo ndipo anati, Uyo ndi mbuyanga: chifukwa chake namwali anatenga chophimba chake nadziphimba. Mnyamatayo ndipo anamuuza Isaki zonse anazichita. Ndipo Isaki anamlowetsa mkaziyo m'hema wa amake Sara, namtenga Rebeka, nakhala iye mkazi wake; ndipo anamkonda iye; ndipo Isaki anatonthozedwa mtima atafa amake. Ndipo Abrahamu anatenga mkazi wina dzina lake Ketura. Ndipo anambalira iye Zimirani ndi Yokisani ndi Medani, ndi Midiyani, ndi Isibaki, ndi Suwa. Ndipo Yokisani anabala Sheba, ndi Dedani. Ana a Dedani ndi Aasuri, ndi Aletusi, ndi Aleumi. Ana a Midiyani: Efa, ndi Efere, ndi Hanoki, ndi Abida, ndi Elida. Onse amenewa ndi ana a Ketura. Ndipo Abrahamu anampatsa Isaki zonse anali nazo. Koma kwa ana a akazi ake ang'ono amene Abrahamu anali nao Abrahamu anapatsa mphatso, nawachotsa iwo kwa Isaki mwana wake, akali ndi moyo, kuti anke kum'mawa, ku dziko la kum'mawa. Masiku a zaka za moyo wake wa Abrahamu amene anakhala ndi moyo ndiwo zaka zana limodzi, kudza makumi asanu ndi limodzi, kudza khumi ndi zisanu. Ndipo Abrahamu anamwalira, nafa m'ukalamba wake wabwino, nkhalamba ya zaka zambiri; natengedwa akhale ndi a mtundu wake. Ndipo ana ake Isaki ndi Ismaele anamuika iye m'phanga la Makipela, m'munda wa Efuroni mwana wake wa Zohari Muhiti, umene uli patsogolo pa Mamure; munda umene anagula Abrahamu kwa ana a Hiti: pamenepo anamuika Abrahamu ndi Sara mkazi wake. Ndipo panali atafa Abrahamu, Mulungu anamdalitsa Isaki mwana wake; ndipo Isaki anakhala pa Beere-Lahai-Roi. Mibadwo ya Ismaele mwana wamwamuna wake wa Abrahamu, amene Hagara Mwejipito mdzakazi wa Sara anambalira Abrahamu ndi iyi: ndipo maina a ana a Ismaele, maina ao m'mibadwo yao ndi awa: woyamba wa Ismaele ndi Nebayoti; ndi Kedara, ndi Adibeele, ndi Mibisamu, ndi Misima, ndi Duma, ndi Masa; ndi Hadadi, ndi Tema, ndi Yeturi, ndi Nafisi, ndi Kedema; ana a Ismaele ndi awa: maina ao m'midzi yao, m'misasa yao ndi awa: akalonga khumi ndi awiri m'mitundu yao. Zaka za moyo wa Ismaele ndi izi: zaka zana limodzi kudza makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri: ndipo iye anamwalira, natengedwa akhale ndi a mtundu wake. Ndipo anakhala iwo kuyambira ku Havila kufikira ku Suri, ndiko kum'mawa kwake kwa Ejipito, pakunka ku Asiriya: ndipo iye anakhala pamaso pa abale ake onse. Mibadwo ya Isaki mwana wake wa Abrahamu ndi iyi: Abrahamu anabala Isaki: ndipo Isaki anali wa zaka makumi anai pamene anakwata Rebeka, mwana wamkazi wa Betuele Mwaramu wa ku Padanaramu, mlongo wake wa Labani Mwaramu. Ndipo Isaki anampembedzera mkazi wake kwa Yehova popeza anali wouma: ndipo Yehova analola kupembedza kwake, ndipo Rebeka mkazi wake anatenga pakati. Ndipo ana analimbana m'kati mwake: ndipo iye anati, Ngati chotero, ine ndikhala ndi moyo bwanji? Ndipo ananka kukafunsa kwa Yehova. Yehova ndipo anati kwa iye, Mitundu iwiri ili m'mimba mwako, magulu awiri a anthu adzatuluka m'mimba mwako; gulu lina lidzapambana mphamvu ndi linzake; wamkulu adzakhala kapolo wa wamng'ono. Atatha masiku ake akubala, taonani, amapasa anali m'mimba mwake. Ndipo woyamba anabadwa wofiira, mwake monse monga malaya aubweya; ndipo anamutcha dzina lake Esau. Pambuyo pake ndipo anabadwa mphwake ndipo dzanja lake linagwira chitende cha Esau, ndi dzina lake linatchedwa Yakobo: ndipo Isaki anali wa zaka makumi asanu ndi limodzi pamene mkazi wake anabala iwo. Ndipo anakula anyamatawo; ndipo Esau anali munthu wakudziwa zakusaka nyama, munthu wa m'thengo; ndipo Yakobo anali munthu wofatsa, wakukhala m'mahema. Ndipo Isaki anakonda Esau, chifukwa anadya nyama yake ya m'thengo; koma Rebeka anakonda Yakobo. Ndipo Yakobo anaphika mphodza: ndipo Esau anachokera kuthengo, nalefuka: ndipo Esau anati kwa Yakobo, Undipatse ndidye chofiiracho; chifukwa ndalefuka: chifukwa chake anamutcha dzina lake Edomu. Ndipo Yakobo anati, Tigulane lero ukulu wako. Ndipo Esau anati, Taona, ine ndifuna kufa: ukuluwo ndidzapindulanji nao? Ndipo anati Yakobo, Undilumbirire ine lero lomwe, ndipo analumbirira iye; nagulana ndi Yakobo ukulu wake. Ndipo Yakobo anampatsa Esau mkate ndi mphodza zophika; ndipo iye anadya, namwa, nanyamuka, napita: chomwecho Esau ananyoza ukulu wake. Ndipo panali njala padzikopo, yoyenjezeka ndi njala yoyamba ija imene inali masiku a Abrahamu, ndipo Isaki ananka kwa Abimeleki mfumu ya Afilisti ku Gerari. Ndipo Yehova anamuonekera iye nati, Usatsikire ku Ejipito, khala m'dziko m'mene ndidzakuuza iwe; khala mlendo m'dziko muno, ndipo Ine ndidzakhala ndi iwe, ndipo ndidzadalitsa iwe chifukwa kuti ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako maiko onse awa, ndipo ndidzalimbikitsa chilumbiriro ndinachilumbirira kwa Abrahamu atate wako; ndipo ndidzachulukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, ndipo ndidzapatsa mbeu zako maiko onsewa; m'mbeu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa; chifukwa kuti Abrahamu anamvera mau anga, nasunga chilangizo changa, ndi maweruziro anga, ndi malemba anga ndi malamulo anga. Ndipo Isaki anakhala m'Gerari; ndipo anthu a kumeneko anamfunsa iye za mkazi wake; ndipo iye anati, Ndiye mlongo wanga: chifukwa kuti anaopa kunena, Mkazi wanga; anati, anthu a kumeneko angandiphe ine chifukwa cha Rebeka; popeza anali wokongola pakumuona. Ndipo panali atakhala komwe masiku ambiri, Abimeleki mfumu ya Afilisti, anayang'ana kunja kwa zenera, napenya, taona, Isaki analinkuseka ndi Rebeka mkazi wake. Ndipo Abimeleki anamuitana Isaki nati, Taona, uyo ndi mkazi wako ndithu: kodi bwanji unati, Ndiye mlongo wanga? Ndipo Isaki anati kwa iye, Chifukwa ndinati, Ndingafe chifukwa cha iye. Ndipo Abimeleki anati, Nchiyani chimenechi watichitira ife? Panatsala pang'ono ena a anthu akadagona naye mkazi wako, ndipo ukadatichimwitsa ife. Ndipo Abimeleki anauza anthu ake, nati, Aliyense amene akhudza mwamuna uyo kapena mkazi wake, zoonatu adzaphedwa. Ndipo Isaki anabzala m'dzikomo, nalandira za makumi khumi chaka chimenecho; ndipo Yehova anamdalitsa iye. Ndipo analemera munthuyo, nalemera ndithu kufikira kuti anakhala wolemera kwambiri: ndipo anali ndi chuma cha nkhosa, ndi chuma cha zoweta, ndi banja lalikulu: ndipo Afilisti anamchitira iye nsanje. Ndipo zitsime zonse anakumba anyamata a atate wake, Abrahamuyo akali moyo, Afilisti anazitseka, nazikwirira ndi dothi. Ndipo Abimeleki anati kwa Isaki, Uchoke kwa ife chifukwa kuti iwe uli wamphamvu wopambana ife. Ndipo Isaki anachoka kumeneko, namanga hema wake m'chigwa cha Gerari, nakhala kumeneko. Ndipo Isaki anafukulanso zitsime za madzi, anazikumba masiku a Abrahamu atate wake; chifukwa kuti Afilisti anazitseka atafa Abrahamu: ndipo anazitcha maina monga maina omwe anazitcha atate wake. Ndipo anyamata a Isaki anakumba m'chigwa, napeza kumeneko chitsime cha madzi otumphuka. Ndipo abusa a Gerari anakangana ndi abusa a Isaki kuti, Madzi ndi athu; ndipo anatcha dzina la chitsimecho Eseke: chifukwa anakangana naye. Ndipo anakumbanso chitsime china, ndipo anakangana nachonso; natcha dzina lake Sitina. Ndipo anachoka kumeneko nakumba chitsime china; koma sanakangane nacho chimenecho; ndipo anatcha dzina lake Rehoboti; ndipo anati, Chifukwa kuti tsopano Yehova anatipatsa ife malo, ndipo tidzabalana m'dziko muno. Ndipo anachoka kumeneko nakwera kunka ku Beereseba. Ndipo Yehova anamuonekera iye usiku womwewo, nati, Ine ndine Mulungu wa Abrahamu atate wako; usaope, chifukwa kuti Ine ndili ndi iwe, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kuchulukitsa mbeu zako, chifukwa cha Abrahamu kapolo wanga. Ndipo anamanga kumeneko guwa la nsembe, naitana dzina la Yehova, namanga hema wake kumeneko: ndi pamenepo anyamata a Isaki anakumba chitsime. Ndipo ananka kwa iye Abimeleki kuchokera ku Gerari, ndi Ahuzati bwenzi lake, ndi Fikolo, kazembe wa nkhondo yake. Ndipo Isaki anati kwa iwo, Mwandidzera chifukwa chiyani, inu akundida ine, ndi kundichotsa kwanu? Ndipo iwo anati, Kuona tinaona kuti Yehova ali ndi iwe; ndipo tinati, Tilumbiriranetu tonse awiri, ife ndi iwe, tichite pangano ndi iwe; kuti usatichitire ife zoipa, pakuti sitidakhudza iwe, sitidakuchitira kanthu koma kabwino ndiko, ndipo takulola umuke ndi mtendere; ndiwe tsopano wodalitsidwa ndi Yehova. Ndipo anakonzera iwo madyerero, ndipo anadya namwa. Ndipo analawira m'mamawa nalumbirirana wina ndi mnzake; ndipo Isaki anawalola amuke, ndipo anauka kuchokera kwa iye m'mtendere. Ndipo panali tsiku lomwelo anyamata ake a Isaki anadza namuuza iye za chitsime chimene anakumba, nati kwa iye, Tapeza madzi. Ndipo anatcha dzina lake Siba, chifukwa chake dzina la mudziwo ndi Beereseba kufikira lero lino. Pamene Esau anali wa zaka makumi anai, anakwatira Yuditi mwana wamkazi wa Beeri Muhiti, ndi Basemati mwana wamkazi wa Eloni Muhiti: ndipo iwo anapweteka mtima wa Isaki ndi wa Rebeka. Ndipo panali atakalamba Isaki, ndi maso ake anali akhungu losaona nalo, anamuitana Esau mwana wake wamwamuna wamkulu, nati kwa iye, Mwana wanga; ndipo anati kwa iye, Ndine pano. Ndipo anati, Taonatu, ndakalamba, sindidziwa tsiku la kufa kwanga: Tsopano tengatu zida zako ndi phodo lako ndi uta wako, numuke kuthengo kundisakira ine nyama: nundikonzere ine chakudya chokolera chonga chomwe ndichikonda ine, nudze nacho kwa ine kuti ndidzadye; kuti moyo wanga ukadalitse iwe ndisanafe. Ndipo anamva Rebeka pamene Isaki ananena ndi Esau mwana wake. Ndipo Esau ananka kuthengo kukasaka nyama ndi kubwera nayo. Ndipo Rebeka ananena kwa Yakobo mwana wake, nati, Taona ndinamva atate wako alimkunena ndi Esau mkulu wako kuti, Unditengere ine nyama, undikonzere ine chakudya chokolera, kuti ndidzadye, ndi kudalitsa iwe pamaso pa Yehova, ndisanafe. Tsopanotu mwana wanga, tamvera mau anga monga momwe nditi ndikuuze iwe. Pitatu kubusa, ukanditengere ine kumeneko tiana tiwiri tabwino tambuzi; ndikonzere nato chakudya chokolera cha atate wako chonga chomwe achikonda: ndipo udzapita nacho kwa atate wako, kuti adye, ndi kukudalitsa iwe asanafe. Yakobo ndipo anati kwa Rebeka amake, Taonani, Esau mkulu wanga ndiye munthu waubweya, ine ndine munthu wosalala. Kapena atate wanga adzandiyambasa, ndipo ndidzaoneka pamaso pake ngati wakunyenga; pamenepo ndidzadzitengera ine temberero, si mdalitso. Ndipo amake anati kwa iye, Pa ine likhale temberero lako mwana wanga; koma tamvera mau anga, kazimuka kunditengera timeneto. Ndipo anamuka nakatenga nadza nato kwa amake; amake ndipo anakonza chakudya chokolera chonga chimene anachikonda atate wake. Ndipo Rebeka anatenga zovala zokoma za Esau mwana wake wamkulu zinali m'nyumba, naveka nazo Yakobo mwana wake wamng'ono; ndipo anaveka zikopa za tiana tambuzi pamanja ake ndi pakhosi pake posalala; ndipo anapereka m'dzanja la mwana wake Yakobo chakudya chokoleracho, ndi mikate imene anaipanga. Ndipo iye analowa kwa atate wake, nati, Atate wanga; iye anati, Ndine pano; ndani iwe mwana wanga? Ndipo Yakobo anati kwa atate wake, Ndine Esau mwana wanu wamkulu; ndachita monga mwandiuza ine; ukanitu, khalani tsonga, idyani nyama yanga kuti moyo wanu undidalitse ine. Ndipo Isaki anati kwa mwana wake, Unaipeza msanga bwanji mwana wanga? Ndipo anati, Chifukwa kuti Yehova Mulungu wanu anandiyendetsa ine bwino. Ndipo Isaki anati kwa Yakobo, Sendera kuno, ndikuyambase mwana wanga, ngati ndiwe mwana wanga Esau ndithu, kapena wina. Ndipo Yakobo anasendera kwa Isaki atate wake, ndipo anamyambasa nati, Mau ndi mau a Yakobo, koma manja ndi manja a Esau. Ndipo sanamzindikire iye, chifukwa kuti manja ake anali aubweya, onga manja a Esau mkulu wake; ndipo anamdalitsa iye. Ndipo anati, Kodi ndiwe mwana wanga weniweni Esau? Ndipo anati, Ndine amene. Ndipo iye anati, Usendere nayo kwa ine, ndidye nyama ya mwana wanga, kuti moyo wanga ukudalitse iwe. Ndipo anasendera nayo kwa iye, nadya iye; ndipo anamtengera vinyo, namwa iye. Ndipo Isaki atate wake anati kwa iye, Senderatu, undimpsompsone mwana wanga. Ndipo anasendera nampsompsona; ndipo anamva kununkhira kwa zovala zake, namdalitsa, nati, Taona, kununkhira kwa mwana wanga, kufanana ndi kununkhira kwa munda anaudalitsa Yehova; Mulungu akupatse iwe mame a kumwamba, ndi zonenepa za dziko lapansi, ndi tirigu wambiri ndi vinyo. Anthu akutumikire iwe, mitundu ikuweramire iwe; uchite ufumu pa abale ako, ana a amai ako akuweramire iwe. Wotemberereka aliyense akutemberera iwe, wodalitsika aliyense akudalitsa iwe. Ndipo panali atatha Isaki kumdalitsa Yakobo, atatuluka Yakobo pamaso pa Isaki atate wake, Esau mkulu wake analowa kuchokera kuthengo. Ndipo iyenso anakonza chakudya chokolera, nadza nacho kwa atate wake, nati kwa atate wake, Auke atate wanga, adye nyama ya mwana wake, kuti moyo wanu undidalitse ine. Ndipo Isaki atate wake anati kwa iye, Ndiwe yani? Ndipo iye anati, Ndine mwana wanu woyamba Esau. Ndipo Isaki ananthunthumira ndi kunthunthumira kwakukulu, nati, Ndani uja anatenga nyama, nadza nayo kwa ine, ndipo ndadyako zonse usadalowe iwe, ndipo ndamdalitsa iye? Inde, adzadalitsika. Pamene Esau anamva mau a atate wake Isaki, analira ndi kulira kwakukulu ndi kowawa kopambana, nati kwa atate wake, Mundidalitse ine, inenso atate wanga. Ndipo iye anati, Mphwako anadza monyenga, nalanda mdalitso wako. Ndipo iye anati, Kodi si ndicho chifukwa anamutcha dzina lake Yakobo? Kuti wandinyenga ine kawiri aka; analanda ukulu wanga ndipo taonani, tsopano walanda mdalitso wanga. Ndipo anati, Kodi simunandisungira ine mdalitso? Ndipo anayankha Isaki nati kwa Esau, Taona, ndamuyesa iye mkulu wako, ndi abale ake onse ndampatsa iye akhale akapolo ake; ndakhazikitsa iye ndi tirigu ndi vinyo; nanga pamenepo mwana wanga, ndidzakuchitira iwe chiyani? Ndipo Esau anati kwa atate wake, Kodi muli nao mdalitso umodzi wokha, atate wanga? Mundidalitse ine, inenso, atate wanga. Ndipo Esau anakweza mau ake nalira. Ndipo Isaki atate wake anayankha nati kwa iye, Taona, pokhala pako mpa zonenepa za dziko lapansi, pa mame a kumwamba akudzera komwe. Udzakhala ndi moyo ndi lupanga lako, nudzakhala kapolo wa mphwako. Ndipo padzakhala pamene udzapulumuka, udzachotsa goli lake pakhosi pako. Ndipo Esau anamuda Yakobo chifukwa cha mdalitso umene atate wake anamdalitsa nao: ndipo Esau anati m'mtima mwake, Masiku a maliro a atate wanga ayandikira; pamenepo ndipo ndidzamupha mphwanga Yakobo. Ndipo anauza Rebeka mau a Esau mwana wake wamkulu: ndipo iye anatumiza naitana Yakobo mwana wake wamng'ono, nati kwa iye, Taona, mkulu wako Esau, kunena za iwe, adzitonthoza yekha mtima wake kuti adzakupha iwe. Ndipo tsopano mwana wanga, tamvera mau anga: tauka, nuthawire kwa Labani mlongo wanga ku Harani; ukhale naye masiku akuwerengeka, mpaka wamchokera ukali wa mkulu wako; mpaka wakuchokera mkwiyo wa mkulu wako, kuti aiwale chimene wamchitira iye; pamenepo ndipo ndidzatumiza kukutenganso iwe kumeneko; ndidzakhala bwanji wopanda inu nonse awiri tsiku limodzi? Ndipo anati Rebeka kwa Isaki, Ndalema moyo wanga chifukwa cha ana akazi a Heti: akatenga Yakobo mkazi wa ana akazi a Heti, onga ana akazi a m'dziko lino, moyo wanga udzandikhalira ine bwanji? Ndipo Isaki anamuitana Yakobo, namdalitsa iye, namuuza iye, nati kwa iye, Usatenge mkazi wa ana akazi a Kanani. Tauka, nupite ku Padanaramu, kunyumba ya Betuele, atate wa amai ako; ukadzitengere mkazi wa kumeneko kwa ana akazi a Labani mlongo wake wa amai ako. Mulungu Wamphamvuyonse akudalitse iwe, akubalitse iwe, akuchulukitse iwe, kuti ukhale khamu la anthu: akupatse iwe mdalitso wa Abrahamu, iwe ndi mbeu zako pamodzi nawe: kuti ulowe m'dziko limene ukhalamo mlendo, limene Mulungu anampatsa Abrahamu. Ndipo Isaki anamlola Yakobo amuke, ndipo ananka ku Padanaramu kwa Labani, mwana wake wa Betuele Mwaramu, mlongo wake wa Rebeka, amai wao wa Yakobo ndi Esau. Ndipo anaona Esau kuti Isaki anamdalitsa Yakobo namtumiza ku Padanaramu kuti atenge mkazi wa kumeneko; ndiponso kuti pamene anamdalitsa iye, anamuuza iye kuti, Usatenge mkazi wa ana akazi a Kanani; ndiponso kuti Yakobo anamvera atate wake ndi amake, nanka ku Padanaramu; ndipo Esau anaona kuti ana akazi a Kanani sanakondweretsa Isaki atate wake: ndipo Esau ananka kwa Ismaele, naonjezera kwa akazi amene anali nao, natenga Mahalati mwana wamkazi wa Ismaele mwana wa Abrahamu, mlongo wake wa Nebayoti akhale mkazi wake. Ndipo Yakobo anachoka m'Beereseba, nanka ku Harani. Ndipo anafika kumalo, nagona kumeneko usiku, chifukwa lidalowa dzuwa: ndipo anatenga mwala wa kumeneko, nauika pansi pa mutu wake, nagona tulo kumeneko. Ndipo analota, taonani, makwerero anaima pansi, pamwamba pake ndipo padafikira kumwamba: ndipo, taonani, amithenga a Mulungu analinkukwera, analinkutsika pamenepo. Taonani, Yehova anaima pamwamba pake, nati, Ine ndine Yehova, Mulungu wa Abrahamu atate wako, ndi Mulungu wa Isaki; dziko limene ulinkugonamo ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako; mbeu zako zidzakhala monga fumbi lapansi, ndipo udzabalalikira kumadzulo ndi kum'mawa ndi kumpoto ndi kumwera: mwa iwe ndi mu mbeu zako mabanja onse a dziko lapansi adzadalitsidwa. Taonani, Ine ndili pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakusunga iwe konse kumene upitako, ndipo ndidzakubwezanso iwe ku dziko lino; chifukwa kuti sindidzakusiya iwe, kufikira kuti nditachita chimene ndanena nawe. Ndipo Yakobo anauka m'tulo take, nati, Ndithu, Yehova ali mommuno; ndipo sindinadziwe. Ndipo anaopa, nati, Poopsa pompano! Pompano ndipo pa nyumba ya Mulungu, si penai, pompano ndipo pa chipata cha kumwamba. Yakobo ndipo anauka m'mamawa, natenga mwala umene anaika pansi pa mutu wake, nauimiritsa, nathira mafuta pamtu pake. Ndipo anatcha dzina la pamenepo Betele; pakuyamba dzina lake la mudziwo ndi Luzi. Yakobo ndipo analumbira chilumbiro, nati, Mulungu akakhala ndi ine, akandisunga ine m'njira imene ndipitamo, akandipatsa ine mkate wa kudya, ndi zovalira za kuvala, kuti ndibwerenso kunyumba ya atate wanga ndi mtendere, pamenepo Yehova adzakhala Mulungu wanga, ndi mwala umenewu ndinauimiritsa, udzakhala nyumba ya Mulungu; ndipo la zonse mudzandipatsa ine, ndidzakupatsani Inu limodzi la magawo khumi. Ndipo Yakobo ananka ulendo wake, nafika ku dziko la anthu a kum'mawa. Ndipo anayang'ana, taonani, chitsime m'dambo, ndipo, taonani, magulu atatu a nkhosa alinkugona kumeneko: pakuti pachitsimepo anamwetsa nkhosa; ndipo mwala wa pakamwa pa chitsime unali waukulu. Kumeneko ndipo zinasonkhana zoweta zonse: ndipo anagubuduza mwala kuuchotsa pakamwa pa chitsime, namwetsa nkhosa, naikanso mwala pakamwa pa chitsime pamalo pake. Ndipo anati Yakobo kwa iwo, Abale anga, ndinu a kuti inu? Nati, Ndife a ku Harani. Ndipo anati kwa iwo, Kodi mumdziwa Labani mwana wake wa Nahori? Nati, Timdziwa. Ndipo anati kwa iwo, Kodi ali bwino? Nati, Ali bwino: taonani, Rakele mwana wake wamkazi alinkudza nazo nkhosa. Ndipo iye anati, Taonani, kukali msana, si nthawi yosonkhanitsa zoweta; mwetsani nkhosa, pitani, kadyetseni. Ndipo anati, Sitingathe, koma zitasonkhana ziweto zonse, ndipo atagubuduza mwala kuuchotsa pakamwa pa chitsime ndiko; pamenepo ndipo tizimwetsa nkhosa. Ali chilankhulire nao, anafika Rakele ndi nkhosa za atate wake, chifukwa anaziweta. Ndipo panali pamene Yakobo anaona Rakele, mwana wamkazi wa Labani, mlongo wake wa amake, ndi nkhosa za Labani mlongo wake wa amake, Yakobo anayandikira nagubuduza kuuchotsa mwala pachitsime, nazimwetsa zoweta za Labani, mlongo wake wa amake. Ndipo Yakobo anampsompsona Rakele nakweza mau ake, nalira. Ndipo Yakobo anamuuza Rakele kuti iye ndiye mbale wake wa atate wake, kuti ndiye mwana wake wa Rebeka, ndipo Rakele anathamanga nakauza atate wake. Ndipo panali pamene Labani anamva mbiri ya Yakobo mwana wa mlongo wake, iye anathamangira kukakomana naye namfungatira, nampsompsona, namlowetsa m'nyumba mwake. Ndipo iye anamfotokozera Labani zinthu zonsezo. Ndipo Labani anati kwa iye, Etu, iwe ndiwe fupa langa ndi thupi langa. Ndipo anakhala naye nthawi ya mwezi umodzi. Ndipo Labani anati kwa Yakobo, Chifukwa iwe ndiwe mbale wanga, kodi udzanditumikira ine kwachabe? Undiuze ine, malipiro ako adzakhala otani? Ndipo Labani anali ndi ana akazi awiri, dzina la wamkulu ndi Leya, dzina la wamng'ono ndi Rakele. Maso a Leya anali ofooka, koma Rakele anali wokoma thupi ndi wokongola. Ndipo Yakobo anamkonda Rakele, nati, Ndidzakutumikirani inu zaka zisanu ndi ziwiri chifukwa cha Rakele mwana wanu wamkazi wamng'ono. Ndipo anati Labani, Kuli kwabwino kuti ndimpatse iwe osampatsa kwa mwamuna wina; ukhalebe ndi ine. Ndipo Yakobo anamtumikira zaka zisanu ndi ziwiri chifukwa cha Rakele; koma zidamuonekera iye ngati masiku owerengeka chifukwa cha chikondi chimene anamkonda iye nacho. Ndipo Yakobo anati kwa Labani, Undipatse ine mkazi wanga, chifukwa masiku anga atha, kuti ndilowe kwa iye. Ndipo Labani anasonkhanitsa anthu onse a kumeneko nakonzera madyerero. Ndipo panali madzulo Labani anatenga Leya mwana wake wamkazi, nadza naye kwa Yakobo, ndipo iye analowa kwa mkaziyo. Ndipo Labani anampatsa mwana wake wamkazi Leya Zilipa mdzakazi wake kuti akhale mdzakazi wa Leya. Ndipo panali m'mamawa, anaona kuti ndi Leya; ndipo anati kwa Labani, Chiyani wandichitira ine? Kodi sindinakutumikira iwe chifukwa cha Rakele? Wandinyenga ine bwanji? Ndipo Labani anati, Satero kwathu kuno, kupatsa wamng'ono asanapatse wamkulu. Umalize sabata lake la uyu, ndipo ndidzakupatsa uyonso chifukwa cha utumiki umene udzanditumikirawo kuonjezera zaka zina zisanu ndi ziwiri. Yakobo ndipo anachita chotero namaliza sabata lake; ndipo Labani anampatsa iye Rakele mwana wake wamkazi kuti akwatire iyenso. Ndipo Labani anampatsa mwana wake wamkazi Rakele Biliha mdzakazi wake kuti akhale mdzakazi wa Rakele. Ndipo Yakobo analowanso kwa Rakele, namkondanso Rakele kopambana Leya, namtumikira Labani zaka zisanu ndi ziwiri zinanso. Pamene Yehova anaona kuti anamuda Leya, anatsegula m'mimba mwake; koma Rakele anali wouma. Ndipo Leya anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Rubeni; pakuti anati, Chifukwa kuti Yehova waona kuvutika kwanga ndipo tsopano mwamuna wanga adzandikonda ine. Ndipo anatenganso pakati, nabala mwana wamwamuna nati, Chifukwa anamva Yehova kuti anandida ine, anandipatsa ine mwana wamwamuna uyunso; ndipo anamutcha dzina lake Simeoni. Ndipo anatenganso pakati nabala mwana wamwamuna, nati, Tsopano lino mwamuna wanga adzadziphatika kwa ine chifukwa ndambalira iye ana amuna atatu; chifukwa chake anamutcha dzina lake Levi. Ndipo anatenganso pakati nabala mwana wamwamuna; nati, Tsopano ndidzamyamikira Yehova; chifukwa chake anamutcha dzina lake Yuda; pamenepo analeka kubala. Pamene Rakele anaona kuti sanambalire Yakobo ana, Rakele anamchitira mkulu wake nsanje; nati kwa Yakobo, Ndipatse ana ndingafe. Ndipo Yakobo anapsa mtima ndi Rakele; nati, Kodi ine ndikhala m'malo a Mulungu amene akukaniza iwe zipatso za mimba? Ndipo Rakele anati, Taonani mdzakazi wanga Biliha, mulowe kwa iye; ndipo iye adzabala pa maondo anga, kuti inenso ndionerepo ana pa iye. Ndipo Rakele anampatsa iye Biliha mdzakazi wake akhale mkazi wake; ndipo Yakobo analowa kwa iye. Ndipo Biliha anatenga pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna. Rakele ndipo anati, Mulungu wandiweruzira ine, namva mau anga, nandipatsa ine mwana; chifukwa chake anamutcha dzina lake Dani. Ndipo Biliha mdzakazi wake wa Rakele anatenganso pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna wachiwiri. Ndipo Rakele anati, Ndi malimbano a Mulungu ndalimbana naye mkulu wanga, ndipo ndapambana naye; ndipo anamutcha dzina lake Nafutali. Pamene Leya anaona kuti analeka kubala, anatenga Zilipa mdzakazi wake, nampatsa iye kwa Yakobo kuti akhale mkazi wake. Ndipo Zilipa mdzakazi wake wa Leya anambalira Yakobo mwana wamwamuna. Ndipo Leya anati, Wamwai ine! Ndipo anamutcha dzina lake Gadi. Ndipo Zilipa mdzakazi wa Leya anambalira Yakobo mwana wamwamuna wachiwiri. Ndipo Leya anati, Ndakondwa ine! Chifukwa kuti ana akazi adzanditcha ine wokondwa: ndipo anamutcha dzina lake Asere. Ndipo Rubeni ananka masiku akudula tirigu, napeza zipatso za mankhwala a chikondi m'thengo, nazitengera kwa amake Leya. Ndipo Rakele anati kwa Leya, Undipatseko mankhwala a mwana wako. Ndipo iye anati kwa Rakele, Kodi mpachabe kuti iwe wachotsa mwamuna wanga? Kodi ufuna kuchotsanso mankhwala a mwana wanga? Rakele ndipo anati, Chifukwa chake iye adzagona nawe usiku uno chifukwa cha mankhwala a mwana wako. Ndipo Yakobo anadza madzulo kuchokera kumunda, ndipo Leya ananka kukomana naye, nati, Ulowe kwa ine chifukwa ndakulipilira iwe ndi mankhwala a mwana wanga. Ndipo anagona naye usiku womwewo. Ndipo Mulungu anamvera Leya, ndipo anatenga pakati, nambalira Yakobo mwana wamwamuna wachisanu. Ndipo Leya anati, Mulungu wandipatsa ine mphotho yanga, chifukwa ndapatsa mdzakazi wanga kwa mwamuna wanga: namutcha dzina lake Isakara. Ndipo Leya anatenganso pakati nambalira Yakobo mwana wamwamuna wachisanu ndi chimodzi. Ndipo Leya anati, Mulungu anandipatsa ine mphatso yabwino; tsopano mwamuna wanga adzakhala ndi ine, chifukwa ndambalira iye ana amuna asanu ndi mmodzi; ndipo anamutcha dzina lake Zebuloni. Pambuyo pake ndipo anabala mwana wamkazi, namutcha dzina lake Dina. Ndipo Mulungu anakumbukira Rakele, ndipo Mulungu anamvera iye, natsegula m'mimba mwake. Ndipo anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, nati, Mulungu wachotsa manyazi anga; namutcha dzina lake Yosefe; ndipo anati, Yehova anandionjezera ine mwana wamwamuna wina. Ndipo panali pamene Rakele anabala Yosefe, Yakobo anati kwa Labani, Undisudzule ine ndinke kwathu ku dziko langa. Undipatse ine akazi anga ndi ana anga chifukwa cha iwowa ndakutumikira iwe, ndimuke: chifukwa udziwa iwe ntchito imene ndinakugwirira iwe. Ndipo Labani anati kwa iye, Ngatitu ndikapeza ufulu pamaso pako, ukhale, chifukwa ndazindikira kuti Yehova wandidalitsa ine chifukwa cha iwe. Ndipo iye anati, Undipangire ine malipiro ako, ndipo ndidzakupatsa. Ndipo iye anati kwa Labani, Udziwa iwe chomwe ndakutumikira iwe ndi chomwe zachita zoweta zako ndi ine. Chifukwa ndisadafike ine, iwe unali nazo zowerengeka, ndipo zachuluka zambirimbiri; Yehova wakudalitsa iwe kulikonse ndinayendako: tsopano ndidzamanga liti banja langa? Ndipo iye anati, Ndikupatsa iwe bwanji? Ndipo Yakobo anati, Usandipatse ine kanthu; ukandichitira ine chotero, ine ndidzadyetsanso ndi kusunganso ziweto zako. Ndidzapita ine lero pakati pa ziweto zonse kusankhasankha m'menemo zoweta zonse zamathothomathotho ndi zamawangamawanga, ndi za nkhosa zonse, ndi mbuzi zonse zamawangamawanga ndi zamathothomathotho: zotero zidzakhala malipiro anga. Chotero chilungamo changa chidzandivomereza m'tsogolo pamene udzandifika chifukwa cha malipiro amene ali patsogolo pako: iliyonse yosakhala yamathothomathotho ndi yamawangamawanga ya mbuzi, ndi iliyonse ya nkhosa yosakhala yakuda, ikapezedwa ndi ine, udzaiyesa yakuba. Ndipo Labani anati, Taona, kukhale monga mau ako. Tsiku lomwelo Labani anachotsa atonde amene anali amipyololomipyololo ndi amathothomathotho, ndi mbuzi zazikazi zinali zamawangamawanga ndi zamathothomathotho zonse zinali zoyera pang'ono, ndi zakuda zonse za nkhosa, napatsa m'dzanja la ana ake amuna. Ndipo iye yekha anatalikitsana ndi Yakobo ulendo wa masiku atatu: ndipo Yakobo anadyetsa ziweto zina za Labani. Ndipo Yakobo anatenga nthyole za mtengo wowisi walibne, ndi za mtengo wakatungurume, ndi za mtengo waarimoni, nakupula m'menemo mizere yoyera, naonetsa moyera mwa m'nthyolemo. Ndipo anaimitsa nthyole zimene anazikupula pandunji ndi zoweta m'michera yakumwera, m'mene ziweto zinafika kumweramo ndipo zidatenga mabere pamene zinadza kumwa. Ndipo ziweto zinatenga mabere patsogolo pa nthyolezo, ndipo zoweta zinabala zamipyololomipyololo, ndi mathothomathotho, ndi zamawangamawanga. Ndipo Yakobo analekanitsa anaankhosa naziika pa zoweta za kuti ziyang'anire zamipyololomipyololo, ndi zakuda zonse za m'zoweta za Labani. Ndipo panali pamene zoweta zolimba zidatenga mabere, Yakobo anaika nthyole pamaso pa zoweta m'micheramo kuti zitenge mabere pa nthyolezo. Koma pamene ziweto zinali zofooka, sanaziike zimenezo: ndipo zofooka, zinali za Labani, ndi zolimba zinali za Yakobo. Munthuyo ndipo analemera kwambiri, nali nazo zoweta zambiri, ndi akapolo aamuna ndi aakazi, ndi ngamira, ndi abulu. Ndipo anamva mau a ana ake a Labani kuti, Yakobo watenga zonse za atate wathu; m'zinthu zinali za atate wathu wapeza iye chuma ichi chonse. Ndipo Yakobo anaona nkhope ya Labani, taonani, siinamuonekera iye monga kale. Ndipo Yehova anati kwa Yakobo, Bwera ku dziko la atate wako, ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakhala ndi iwe. Ndipo Yakobo anatumiza naitana Rakele ndi Leya adze kubusa ku zoweta zake, ndipo anati kwa iwo, Ndiona ine nkhope ya atate wanu kuti siindionekera ine monga kale; koma Mulungu wa atate wanga anali ndi ine. Ndipo inu mudziwa kuti ndi mphamvu zanga zonse ndatumikira atate wanu. Ndipo atate wanu wandinyenga ine, nasinthanitsa malipiro anga kakhumi; koma Mulungu sanamlole iye andichitire ine choipa. Akati chotero, Zamathothomathotho zidzakhala malipiro ako, zoweta zonse zinabala zamathothomathotho; ndipo akati iye chotere, Zamipyololomipyololo zidzakhala malipiro ako, ziweto zonse zinabala mipyololomipyololo. Chomwecho Mulungu anazichotsa zoweta za atate wanu, nandipatsa ine. Ndipo panali potenga mabere ziwetozo, ine ndinatukula maso anga, ndipo ndinapenya m'kulota, taonani, atonde okwera ziweto anali amipyololomipyololo, amathothomathotho, ndi amawangamawanga. Mthenga wa Mulungu ndipo anati kwa ine m'kulotamo, Yakobo; nati ine, Ndine pano. Ndipo anati, Tukulatu maso ako, nuone, atonde onse amene akwera zoweta ali amipyololomipyololo, amathothomathotho, ndi amawangamawanga: chifukwa ndaona zonse zimene Labani akuchitira iwe. Ine ndine Mulungu wa ku Betele, kuja unathira mafuta pamwala paja, pamene unandilumbirira ine chilumbiriro: tsopano uka, nuchoke m'dziko lino, nubwerere ku dziko la abale ako. Ndipo Rakele ndi Leya anayankha, nati kwa iye, Kodi tili nalonso gawo kapena cholowa m'nyumba ya atate wathu? Kodi satiyesa ife alendo? Chifukwa anatigulitsa ife, nathanso kuononga ndalama zathu. Chifukwa kuti chuma chonse Mulungu anachichotsa kwa atate wathu ndi chathu ndi cha ana athu; tsono, zonse wakunenera iwe Mulungu, uchite. Ndipo anauka Yakobo nakweza ana ake ndi akazi ake pa ngamira; ndipo ananka nazo zoweta zake zonse, ndi chuma chake chonse anachisonkhanitsa, zoweta zake anaziona m'Padanaramu, kuti anke kwa Isaki atate wake ku dziko la Kanani. Ndipo Labani ananka kukasenga nkhosa zake: ndipo Rakele anaba aterafi a atate wake. Ndipo Yakobo anathawa kwa Labani Mwaramu mobisika, m'mene sanamuuze iye kuti analinkuthawa. Ndipo anathawa iye ndi zonse anali nazo: ndipo anauka naoloka panyanja naloza nkhope yake iyang'anire kuphiri la Giliyadi. Tsiku lachitatu anamuuza Labani kuti Yakobo wathawa. Ndipo iye anatenga abale ake pamodzi naye, namlondola iye ulendo wa masiku asanu ndi awiri: nampeza iye paphiri la Giliyadi. Ndipo Mulungu anadza kwa Labani Mwaramu usiku, nati kwa iye, Tadziyang'anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa. Ndipo Labani anakomana naye Yakobo. Ndipo Yakobo anamanga hema wake m'phirimo: ndipo Labani ndi abale ake anamanga m'phiri la Giliyadi. Ndipo Labani anati kwa Yakobo, Wachitanji? Wathawa kwa ine mobisika ndi kutenga ana anga akazi, monga mikoli ya lupanga. Wathawanji iwe mobisika, ndi kundichokera kuseri, osandiuza ine, kuti ndikadakumukitsa iwe ndi kusekerera ndi nyimbo ndi lingaka ndi zeze? Ndipo sunandiloleza ine ndimpsompsone ana anga aamuna ndi aakazi? Wapusa iwe pakuchita chotero. M'dzanja langa muli mphamvu yakuchitira iwe zoipa koma Mulungu wa atate wako anati kwa ine usiku walero, kuti, Tadziyang'anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa. Tsono ungakhale ukadamuka chifukwa mtima wako ulinkukhumba nyumba ya atate wako, bwanji waba iwe milungu yanga? Ndipo anayankha Yakobo nati kwa Labani, Chifukwa ndinaopa: chifukwa kuti, ndinati, Kapena udzandilanda ine ana ako akazi. Aliyense umpeza ali nayo milungu yako, asakhale ndi moyo: pamaso pa abale athu, tayang'anira zako zili ndi ine, nuzitenge wekha. Pakuti sanadziwe Yakobo kuti Rakele anaiba. Ndipo Labani analowa m'hema wa Yakobo, ndi m'hema wa Leya, ndi m'mahema a adzakazi awiri aja; koma sanapeze. Ndipo anatuluka m'hema wa Leya nalowa m'hema wa Rakele. Ndipo Rakele anatenga aterafiwo nabisa pa chokhalira cha ngamira, nakhala pamenepo. Ndipo Labani anafunafuna m'hema monse, koma sanawapeze. Ndipo Rakele anati kwa atate wake, Asakwiye mbuyanga kuti sindingathe kuuka pamaso panu; chifukwa zochitika pa akazi zili pa ine. Ndipo Labani anafunafuna koma sanapeze aterafiwo. Ndipo anakwiya Yakobo namkalipira Labani: ndipo Yakobo anayankha nati kwa Labani, Kodi ndachimwa chiyani? Uchimo wanga nguti, kuti unanditsatatsata ine pambuyo panga? Pakuti wafunafuna monse ndili nazo, kodi wapeza chiyani pa zinthu za m'nyumba mwako? Tafika nacho apa pa abale anga ndi ako, kuti aweruze pa ife tonse awiri. Zaka makumi awiriwo ndakhala nawe, nkhosa ndi mbuzi zako zazikazi sizinapoloze, ndi abira a zoweta zako sindinadye. Chimene chinazomoledwa ndi chilombo sindinachitengere kwa iwe; ndekha ndinalipira; pa dzanja langa unachifuna, chingakhale chobedwa kapena pausiku kapena pausana. Chotero ndinakhala; usana ludzu linakomola ine, usiku chisanu; tulo tanga tinachoka m'maso mwanga. Ndinakhala chotere zaka makumi awiri m'nyumba mwako; zaka khumi ndi zinai ndinakutumikira iwe chifukwa cha ana ako akazi awiri, ndi zaka zisanu ndi chimodzi chifukwa cha zoweta zako; wasintha malipiro anga kakhumi. Mulungu wa atate wanga, Mulungu wa Abrahamu, ndi Kuopsa kwa Isaki zikadapanda kukhala ndi ine, ukadandichotsa ine wopanda kanthu m'manja. Mulungu anakuona kusauka kwanga, ndi ntchito ya manja anga, ndipo anadzudzula iwe usiku walero. Ndipo Labani anayankha nati kwa Yakobo, Akaziwa ndiwo ana anga, anawa ndiwo ana anga, zowetazi ndizo zoweta zanga ndi zonse ulinkuziona ndizo zanga: nanga ndidzachitira ine chiyani lero kwa ana anga akazi amenewa, kapena ana ao amene anabala? Tsopano tiyeni tipangane pangano, ine ndi iwe; likhale mboni pakati pa ine ndi iwe. Ndipo Yakobo anatenga mwala, nauimiritsa. Ndipo Yakobo anati kwa abale ake, Sonkhanitsani miyala; ndipo anasonkhanitsa miyala nakundika mulu: ndipo anadya pamulupo. Ndipo Labani anatcha pamenepo Yegara-Sahaduta; koma Yakobo anatcha Galedi. Ndipo Labani anati, Muluwu ndiwo mboni pakati pa ine ndi iwe lero. Chifukwa chake anatcha dzina lake, Galedi; ndi Mizipa, chifukwa kuti anati, Yehova ayang'anire pakati pa ine ndi iwe, pamene tisiyana wina ndi mnzake. Ukasautsa ana anga akazi, kapena ukatenga akazi kuonjezera pa ana anga, palibe munthu mmodzi ali nafe; taonani, Mulungu ndiye mboni yanga ndi yako. Ndipo Labani anati kwa Yakobo. Taona muluwu, taona choimiritsachi, ndachiimiritsa pakati pathu. Muluwu ndiwo mboni, choimiritsachi ndicho mboni, kuti ine sindidzapitirira pa muluwu kunka kwa iwe, ndipo iwe sudzapitirira pa muluwu ndi pa choimiritsachi kudza kwa ine kuti tichitirane zoipa. Mulungu wa Abrahamu ndi Mulungu wa Nahori, Mulungu wa atate wao aweruze pa ife. Ndipo Yakobo analumbirira pa Kuopsa kwa atate wake Isaki. Ndipo Yakobo anapereka nsembe paphiripo, naitana abale ake kuti adye chakudya; ndipo anadya chakudya, nagona paphiripo usiku wonse. M'mamawa Labani anauka nampsompsona ana ake aamuna ndi aakazi, nawadalitsa: ndipo Labani anachoka, nabwera kumalo kwake. Ndipo Yakobo anankabe ulendo wake, ndipo amithenga a Mulungu anakomana naye. Pamene Yakobo anawaona anati, Ili ndi khamu la Mulungu: ndipo anatcha pamenepo dzina lake Mahanaimu. Ndipo Yakobo anatumiza amithenga patsogolo pake kwa Esau mkulu wake, ku dziko la Seiri, kudera la ku Edomu. Ndipo anauza iwo kuti, Mukanene chotere kwa mbuyanga Esau: Atero Yakobo kapolo wako, ndakhala pamodzi naye Labani, ndipo ndakhalabe kufikira tsopano lino: ndipo ndili nazo ng'ombe ndi abulu, ndi zoweta ndi akapolo ndi adzakazi, ndipo ndatumiza kukuuza mbuyanga kuti ndipeze ufulu pamaso pako. Ndipo amithenga anabwera kwa Yakobo kuti, Tidafika kwa mbale wanu Esau, ndipo iyenso alinkudza kukomana nanu, ndipo ali nao anthu mazana anai. Ndipo Yakobo anaopa kwambiri, navutidwa; ndipo anagawa anthu anali nao ndi nkhosa ndi zoweta, ndi ngamira, zikhale makamu awiri; ndipo anati, Akafika Esau pa khamu limodzi nalikantha, linalo lotsala lidzapulumuka. Ndipo Yakobo anati, Mulungu wa atate wanga Abrahamu, Mulungu wa atate wanga Isaki, Yehova, amene munati kwa ine, Bwera ku dziko lako, ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakuchitira iwe bwino: sindiyenera zazing'ono za zifundo zonse, ndi zoona zonse, zimene mwamchitira kapolo wanu: chifukwa ndindodo yanga ndinaoloka pa Yordani uyu; ndipo tsopano ndili makamu awiri. Mundipulumutsetu ine m'dzanja la mkulu wanga, m'dzanja la Esau; chifukwa ine ndimuopa iye, kapena adzadza kudzandikantha ine, ndi amai pamodzi ndi ana. Ndipo Inu munati, Ndidzakuchitira iwe bwino ndithu, ndidzakuyesa mbeu yako monga mchenga wa pa nyanja, umene sungathe kuwerengeka chifukwa cha unyinji wake. Ndipo anagona komweko usiku womwewo, natengako zimene anali nazo, mphatso yakupatsa Esau mkulu wake: mbuzi zazikazi mazana awiri, atonde makumi awiri, nkhosa zazikazi mazana awiri, ndi zazimuna makumi awiri, ngamira zamkaka makumi atatu ndi ana ao, ng'ombe zazikazi makumi anai, zazimuna khumi, abulu akazi makumi awiri ndi ana khumi. Ndipo anazipereka zimenezo m'manja a anyamata ake, gulu pa lokha gulu pa lokha: ndipo anati kwa anyamata ake, Taolokani patsogolo panga, tachitani danga pakati pa magulu, lina ndi lina. Ndipo anauza wotsogolera kuti, Pamene akomana nawe mkulu wanga Esau ndi kufunsa iwe kuti, Ndiwe yani, umuka kuti? Za yani zimenezi patsogolo pako? Pomwepo uziti, Za kapolo wanu Yakobo; ndizo mphatso yotumizidwa kwa mbuyanga Esau; taonani ali pambuyo pathu. Ndipo anauzanso wachiwiri ndi wachitatu, ndi onse anatsata magulu, kuti, Muzinena kwa Esau chotero, pamene mukomana naye: ndiponso muziti, Ndiponso, taonani, kapolo wanu Yakobo ali pambuyo pathu. Pakuti anati, Ndidzampembedzera iye ndi mphatso imene ipita patsogolo panga, pambuyo pake ndidzaona nkhope yake; kapena adzandilandira ine. Momwemo naolotsa mphatso patsogolo pake: ndipo iye yekha anagona usiku womwewo pachigono. Ndipo anauka usiku womwewo, natenga akazi ake awiri, ndi adzakazi ake awiri, ndi ana ake amuna khumi ndi mmodzi, naoloka pa dooko la Yaboki. Ndipo anawatenga iwo nawaolotsa pamtsinje, naziolotsa zonse anali nazo. Ndipo anatsala Yakobo yekha; ndipo analimbana naye munthu kufikira mbandakucha. Ndipo pamene anaona kuti sanamgonjetsa, anakhudza nsukunyu ya ntchafu yake; ndipo nsukunyu ya ntchafu yake ya Yakobo inaguluka, pakulimbana naye. Ndipo iye anati Ndileke ndimuke, chifukwa kulinkucha. Ndipo Yakobo anati, Sindidzakuleka iwe kuti umuke, ukapanda kundidalitsa ine. Ndipo iye anati kwa Yakobo, Dzina lako ndani? Nati iye, Yakobo. Ndipo anati, Dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma Israele, chifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana. Yakobo ndipo anafunsa iye, nati, Undiuze ine dzina lako. Ndipo iye anati, Undifunsa dzina chifukwa ninji? Ndipo anamdalitsa iye pamenepo. Ndipo Yakobo anatcha dzina la malo amenewo, Penuwele: chifukwa ndaonana ndi Mulungu nkhope ndi nkhope, ndipo wapulumuka moyo wanga. Ndipo kudamchera iye pamene anaoloka pa Penuwele, ndipo iye anatsimphina ndi ntchafu yake. Chifukwa chake ana a Israele samadya mtsempha ya thako ili pa nsukunyu ya ntchafu kufikira lero: chifukwa anakhudza nsukunyu ya ntchafu ya Yakobo pa mtsempha ya thako. Ndipo Yakobo anatukula maso ake, taonani, anadza Esau, ndi pamodzi naye anthu mazana anai. Ndipo anagawira ana kwa Leya, ndi kwa Rakele, ndi kwa adzakazi awiri aja. Ndipo anaika adzakazi ndi ana ao patsogolo, ndi Leya ndi ana ake pambuyo pao, ndi Rakele ndi Yosefe pambuyo pa onse. Ndipo iye mwini anatsogolera patsogolo pao, nawerama pansi kasanu ndi kawiri mpaka anayandikira mkulu wake. Ndipo Esau anathamangira kukomana naye namfungatira, nagwa pankhope pake, nampsompsona; ndipo analira iwo. Ndipo anatukula maso ake nawaona akazi ndi ana; nati, Ndani awa ali ndi iwe? Ndipo iye anati, Ndiwo ana amene Mulungu anakomera mtima kumpatsa kapolo wanu. Ndipo adzakazi anayandikira ndi ana ao, nawerama pansi. Ndiponso Leya ndi ana ake anayandikira nawerama pansi: pambuyo pake anayandikira Yosefe ndi Rakele, nawerama pansi. Ndipo anati, Nanga khamu lonse limene ndinakomana nalo nlotani? Ndipo anati, Kuti ndipeze ufulu pamaso pa mbuyanga. Ndipo Esau anati, Zanga zindifikira; mbale wanga, khala nazo zako iwe wekha. Ndipo Yakobo anati, Iaitu, ngatitu ndapeza ufulu pamaso panu, mulandire mphatso yanga pa dzanja langa; pakuti popeza ndinaona nkhope yanu, monga anthu aona nkhope ya Mulungu, ndipo inu mwandivomereza ine. Landiranitu mdalitso wanga umene wafika kwa inu, pakuti Mulungu wandichitira ine zaufulu, ndipo zanganso zindifikira. Ndipo anamkakamiza, nalandira. Ndipo Esau anati, Tiyeni timuke; nditsogolera ndine. Ndipo anati kwa iye, Mbuyanga adziwa kuti ana ali ambowa, ndipo nkhosa ndi zoweta ndili nazo zilinkuyamwitsa: ndipo akathamangitsa tsiku limodzi zoweta zonse zidzafa. Mbuyanga atsogoleretu kapolo wake, ndipo ine ndidzazitsogolera pang'onopang'ono monga mwa mayendedwe a zoweta zili pamaso panga, ndi monga mwa mayendedwe a ana, mpaka ndifike kwa mbuyanga ku Seiri. Ndipo Esau anati, Ndikusiyire anthu ena amene ali ndi ine. Ndipo iye anati, Chifukwa chanji? Ndipeze ine ufulu pamaso pa mbuyanga. Ndipo Esau anabwera tsiku lomwelo kunka ku Seiri. Ndipo Yakobo anankabe ulendo wake ku Sukoti, namanga nyumba yake pamenepo, namanga makola a zoweta zake: chifukwa chake dzina lake la kumeneko ndi Sukoti. Ndipo Yakobo anafika ndi mtendere kumudzi wa Sekemu umene uli m'dziko la Kanani, pamene anachokera ku Padanaramu; namanga tsasa pandunji pa mudzipo. Ndipo anagula ndi ndalama zana limodzi dera la munda kumeneko anamanga hema wake, pa dzanja la ana ake a Hamori atate wake wa Sekemu. Ndipo anamanga pamenepo guwa la nsembe, natcha pamenepo El-Elohe-Israele. Ndipo Dina mwana wamkazi wa Leya, amene anambalira Yakobo, ananka kukaona akazi a kumeneko. Pamene anamuona iye Sekemu, mwana wake wamwamuna wa Hamori Muhivi, kalonga wa dzikolo, anamtenga nagona ndi iye, namuipitsa. Ndipo mtima wake unakhumba Dina mwana wake wamkazi wa Yakobo, ndipo anamkonda namwaliyo, nanena momkopa namwaliyo. Ndipo anati Sekemu kwa atate wake Hamori kuti, Munditengere ine mkazi uyo akhale mkazi wanga. Ndipo anamva Yakobo kuti anamuipitsa Dina, mwana wake wamkazi; ana ake amuna anali ndi zoweta zake kudambo: ndipo Yakobo anakhala chete mpaka anafika iwo. Ndipo Hamori atate wake wa Sekemu anatuluka kunka kwa Yakobo kukanena ndi iye. Ndipo pakumva icho ana ake amuna a Yakobo anabwera pochokera kudambo: amunawo ndipo anapwetekwa mtima, nakwiya kwambiri, chifukwa iyeyo anachita chopusa choipira Israele pakugona ndi mwana wamkazi wa Yakobo; ndicho chosayenera kuchita. Ndipo Hamori ananena ndi iwo, kuti, Mtima wa Sekemu mwana wanga umkhumba mwana wako wamkazi: umpatsetu kuti akhale mkazi wake. Mukwatirane ndi ife: tipatseni ife ana anu akazi, ndiponso dzitengereni ana athu akazi. Ndipo mudzakhala pamodzi ndi ife, dziko lidzakhala pamaso panu; khalani m'menemo ndi kuchita malonda, ndi kukhala nazo zanuzanu m'menemo. Ndipo Sekemu anati kwa atate wake wa mkazi ndi kwa abale ake, Tipeze ufulu pamaso panu, chimene mudzanena kwa ine ndidzapereka. Mundipemphe ine za mitulo ndi zaulere zambirimbiri, ndipo ndidzapereka monga mudzanena kwa ine; koma mundipatse ine namwaliyo akhale mkazi wanga. Ndipo ana ake amuna a Yakobo anayankha Sekemu ndi Hamori atate wake monyenga, nanena, popeza anamuipitsa Dina mlongo wao, nati kwa iwo, Sitingathe kuchita ichi, kupereka mlongo wathu kwa mwamuna wosadulidwa; chifukwa kumeneko ndiko kutichepetsa ife. Koma apa pokha tidzakuvomerezani: ngati mudzakhala onga ife ndi kudulidwa amuna onse; pamenepo tidzakupatsani inu ana athu akazi, ndipo tidzadzitengera ana anu akazi, ndipo tidzakhala pamodzi ndi inu, ndi kukhala mtundu umodzi. Koma mukapanda kutimvera ndi kusadulidwa, pamenepo tidzatenga mwana wathu wamkazi, ndi kumuka naye. Mau ao ndipo anakomera Hamori ndi Sekemu mwana wake wa Hamori. Ndipo mnyamatayo sanachedwe kuchichita popeza anakondwera ndi mwana wake wamkazi wa Yakobo; ndipo iye anali wolemekezedwa woposa onse a pa banga la atate wake. Ndipo Hamori ndi Sekemu mwana wake anafika ku chipata cha mudzi wao, nalankhulana ndi anthu a mudzi wao, kuti, Anthu amenewa ali amtendere pamodzi ndi ife; chifukwa chake akhale m'dzikomo, achite malonda m'menemo: pakuti taonani dzikolo lili lalikulu lokwanira iwo; tidzitengere ana ao akazi akhale akazi athu, tiwapatse amenewa ana athu akazi. Anthuwo adzatiloleza ife tikhale nao anthu amodzi, pokhapo amuna onse a mwa ife adzadulidwa, monga iwo adulidwa. Kodi ng'ombe zao ndi chuma chao ndi zoweta zao sizidzakhala zathu? Pokhapo tivomerezana nao ndipo adzakhala pamodzi ndi ife. Ndipo onse amene anatuluka pa chipata cha mudzi wao anamvera Hamori ndi mwana wake Sekemu, nadulidwa amuna onse akutuluka pa chipata cha mudzi wao. Ndipo panali tsiku lachitatu pamene anamva kuwawa, ana amuna awiri a Yakobo, Simeoni ndi Levi, abale ake a Dina, anatenga wina lupanga lake wina lake, nalimbika mtima nalowa m'mudzi napha amuna onse. Ndipo anapha Hamori ndi Sekemu mwana wake ndi lupanga, natulutsa Dina m'nyumba ya Sekemu nachoka naye. Ndipo ana amuna a Yakobo anadza kwa ophedwa nafunkha mudzi chifukwa anamuipitsa mlongo wao. Ndipo analanda nkhosa zao ndi zoweta zao ndi abulu ao, ndi za m'mudzi, ndi za m'munda; ndi chuma chao chonse ndi ana ao ndi akazi ao anawagwira, nafunkha zonse za m'nyumba. Ndipo Yakobo anati kwa Simeoni ndi Levi, Mwandisautsa ndi kundinukhitsa ine mwa anthu okhala m'dzikomu, mwa Akanani ndi mwa Aperizi; ndipo ine ndine wa anthu owerengeka, adzandisonkhanira ine ndi kundikantha: ndipo ndidzapasulidwa ine ndi a pa nyumba yanga. Ndipo iwo anati, Kodi iye ayenera kusandutsa mlongo wathu wadama? Ndipo Mulungu anati kwa Yakobo, Nyamuka nukwere kunka ku Betele nukhale kumeneko: numange kumeneko guwa la nsembe la Mulungu amene anaonekera kwa iwe pamene unathawa ku nkhope ya Esau mbale wako. Ndipo Yakobo anati kwa a banja lake, ndi kwa onse amene anali ndi iye, Chotsani milungu yachilendo ili mwa inu, mudziyeretse, ndi kupindula zovala zanu: tinyamuke, tikwere tinke ku Betele: ndipo tidzamanga kumeneko guwa la nsembe la Mulungu amene anandivomereza tsiku la mavuto anga, ndiponso anali ndi ine m'njira m'mene ndinapitamo. Ndipo anampatsa Yakobo milungu yachilendo yonse inali m'manja mwao, ndi mphete zinali m'makutu mwao: ndipo Yakobo anazibisa pansi pa mtengo wathundu unali pa Sekemu. Ndipo anapita ndipo kuopsa kwa Mulungu kudagwera midzi yakuwazinga, ndipo sanalondole ana a Yakobo. Ndipo Yakobo anafika ku Luzi, ndiko ku dziko la Kanani (ndiwo Betele), iye ndi anthu onse anali pamodzi ndi iye. Ndipo anamanga kumeneko guwa la nsembe, natcha pamenepo El Betele: pakuti kumeneko Mulungu anaonekera kwa iye muja anathawa pa nkhope ya mbale wake. Ndipo anafa Debora mlezi wa Rebeka, naikidwa kunsi kwa Betele, pansi pa mtengo wathundu; ndipo anatcha dzina lake Aloni-Bakuti. Ndipo Mulungu anamuonekeranso Yakobo, pamene iye anachokera m'Padanaramu, namdalitsa iye. Ndipo Mulungu anati kwa iye, Dzina lako ndi Yakobo; dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma dzina lako lidzakhala Israele: ndipo anamutcha dzina lake Israele. Ndipo Mulungu anati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse: ubale, uchuluke; mwa iwe mudzatuluka mtundu ndi gulu la mitundu, ndipo mafumu adzatuluka m'chuuno mwako; ndipo dziko limene ndinapatsa kwa Abrahamu ndi kwa Isaki ndidzalipatsa kwa iwe ndipo ndidzapatsa mbeu zako za pambuyo pako dzikoli. Ndipo Mulungu anakwera kumchokera iye kumene ananena naye. Ndipo Yakobo anaimiritsa mwala pamalo pamene ananena ndi iye, choimiritsa chamwala: ndipo anathira pamenepo nsembe yothira, nathirapo mafuta. Ndipo Yakobo anatcha dzina lake la pamalo pamene Mulungu ananena ndi iye, Betele. Ndipo anachokera ku Betele: ndipo panatsala nthawi asanafike ku Efurata: ndipo Rakele anabala navutidwa. Ndipo panali pamene anavutidwa, namwino anati kwa iye, Usaope: pakuti udzakhala ndi mwana wina wamwamuna. Ndipo pakutsirizika iye, pakuti anamwalira, anamutcha dzina lake Benoni; koma atate wake anamutcha Benjamini. Ndipo anafa Rakele, naikidwa pa njira ya ku Efurata (ndipo Betelehemu). Ndipo Yakobo anaimiritsa mwala pamanda pake: umenewo ndi choimiritsa cha pa manda a Rakele kufikira lero. Ndipo Israele anapita namanga hema wake patseri pa nsanja ya Edere. Ndipo panali pamene Israele anakhala m'dzikomo, Rubeni anamuka nagona ndi Biliha, mkazi wamng'ono wa atate wake: ndipo Israele anamva. Ana amuna a Yakobo anali khumi ndi awiri: ana amuna a Leya: ndiwo Rubeni mwana woyamba wa Yakobo, ndi Simeoni ndi Levi, ndi Yuda, ndi Zebuloni, ndi Isakara; ana amuna a Rakele: ndiwo Yosefe ndi Benjamini; ana amuna a Biliha mdzakazi wake wa Rakele: ndiwo Dani ndi Nafutali; ndipo ana amuna a Zilipa mdzakazi wake wa Leya: ndiwo Gadi ndi Asere: amenewo ndi ana amuna a Yakobo amene anabala iye m'Padanaramu. Ndipo Yakobo anafika kwa Isaki atate wake ku Mamure, ku Kiriyati-Ariba (ndiwo Hebroni) kumene anakhala Abrahamu ndi Isaki. Ndipo masiku a Isaki anali zaka zana limodzi kudza makumi asanu ndi atatu. Ndipo Isaki anatsirizika nafa, nasonkhanitsidwa kwa anthu a mtundu wake, wokalamba ndi wa masiku okwanira: ndipo Esau ndi Yakobo ana ake amuna anamuika iye. Mibadwo ya Esau (ndiye Edomu) ndi iyi: Esau anatenga akazi ake a ana akazi a m'Kanani: Ada mwana wamkazi wa Eloni Muhiti, ndi Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mwana wamkazi wa Zibiyoni Muhivi; ndi Basemati mwana wamkazi wa Ismaele, mlongo wake wa Nebayoti. Ndipo Ada anambalira Esau Elifazi; ndipo Basemati anabala Reuwele; ndipo Oholibama anabala Yeusi, ndi Yalamu, ndi Kora; amenewa ndi ana amuna a Esau, amene anambadwira m'dziko la Kanani. Ndipo Esau anatenga akazi ake, ndi ana ake amuna, ndi ana ake akazi, ndi anthu onse a m'banja mwake, ndi ng'ombe zake, ndi zoweta zake, ndi zonse anali nazo anasonkhanitsa m'dziko la Kanani; ndipo ananka ku dziko losiyana patali ndi Yakobo mphwake. Chifukwa chuma chao chinali chambiri chotero kuti sanakhoze kukhala pamodzi; ndipo dziko lokhalamo iwo silinakhoza kuwakwanira chifukwa cha ng'ombe zao. Ndipo Esau anakhala m'phiri la Seiri; Esau ndiye Edomu. Mibadwo ya Esau atate wao wa Aedomu m'phiri la Seiri ndi iyi: amenewa ndi maina a ana amuna a Esau: Elifazi mwana wamwamuna wa Ada, mkazi wake wa Esau, Reuwele mwana wamwamuna wa Basemati mkazi wake wa Esau. Ndipo ana amuna a Elifazi ndiwo Temani, Omara, Zefo ndi Gatamu, ndi Kenazi. Ndipo Timna anali mkazi wake wamng'ono wa Elifazi mwana wamwamuna wa Esau; ndipo anambalira Elifazi Amaleke: amenewa ndi ana amuna a Ada mkazi wake wa Esau. Ndi ana amuna a Reuwele: Nahati, ndi Zera, Sama, ndi Miza; amenewa ndi ana a Basemati mkazi wake wa Esau. Ana amuna a Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mwana wamkazi wa Zibiyoni, mkazi wake wa Esau, ndi awa: ndipo iye anambalira Esau Yeusi, ndi Yalamu, ndi Kora. Amenewa ndi mafumu a ana amuna a Esau: ana amuna a Elifazi woyamba wa Esau: mfumu Temani, mfumu Omara, mfumu Zefo, mfumu Kenazi, mfumu Kora, mfumu Gatamu, mfumu Amaleke: amenewa ndi mafumu a kwa Elifazi m'dziko la Edomu: amenewa ndi ana amuna a Ada. Amenewa ndi ana amuna a Reuwele mwana wamwamuna wa Esau: mfumu Nahati, mfumu Zera, mfumu Sama, mfumu Miza; amenewa ndi mafumu obadwa kwa Reuwele m'dziko la Edomu: amenewa ndi ana aamuna a Basemati mkazi wake wa Esau. Amenewa ndi ana amuna a Oholibama mkazi wake wa Esau; mfumu Yeusi, mfumu Yalamu, mfumu Kora, amenewa ndi mafumu obadwa kwa Oholibama mwana wamkazi wa Ana, mkazi wake wa Esau. Amenewa ndi ana amuna a Esau, amenewa ndi mafumu ao; yemweyo ndi Edomu. Amenewa ndi ana amuna a Seiri Muhori, okhala m'dzikomo: Lotani ndi Sobala, ndi Zibiyoni, ndi Ana, ndi Disoni ndi Ezere ndi Disani; amenewa ndi mafumu obadwa kwa Ahori, ana a Seiri, m'dziko la Edomu. Ndi ana a Lotani anali Hori ndi Hemani: mlongo wake wa Lotani anali Timna. Ana a Sobala ndi awa: Alivani ndi Manahati ndi Ebala, Sefo ndi Onamu. Ana a Zibiyoni ndi amenewa: Aiya ndi Ana; ameneyo ndiye Ana uja anapeza akasupe a madzi amoto m'chipululu, pakudyetsa abulu a Zibiyoni atate wake. Ana a Ana ndi awa: Disoni ndi Oholibama mwana wamkazi wa Ana. Ana a Disoni ndi awa: Hemudani ndi Esibani ndi Itirani, ndi Kerani. Ana a Ezere ndi awa: Bilihani, ndi Zaavani, ndi Akani. Ana a Disani ndi awa: Uzi ndi Arani. Mafumu obadwa kwa Ahori: mfumu Lotani, mfumu Sobala, mfumu Zibiyoni, mfumu Ana, mfumu Disoni, mfumu Ezere, mfumu Disani; amenewa ndi mafumu obadwa kwa Ahori, monga mwa maufumu ao m'dziko la Seiri. Amenewa ndi mafumu analamulira m'dziko la Edomu, asadalamulire ana a Israele mfumu aliyense. Ndipo Bela mwana wamwamuna wa Beori, analamulira m'Edomu, ndipo dzina la mudzi wake ndilo Dinihaba. Ndipo Bela anamwalira, ndipo Yobabu mwana wamwamuna wa Zera wa ku Bozira analamulira m'malo mwake. Ndipo Yobabu anamwalira, ndipo Husamu wa ku dziko la Atemani analamulira m'malo mwake. Ndipo Husamu anamwalira, ndipo Hadadi mwana wamwamuna wa Bedadi, amene anakantha Midiyani m'dambo la Mowabu, analamulira m'malo mwake: dzina la mudzi wake ndi Aviti. Ndipo Hadadi anamwalira, ndipo Samila wa ku Masireka analamulira m'malo mwake. Ndipo Samila anamwalira, ndipo Shaulo wa ku Rehoboti pambali pa nyanja analamulira m'malo mwake. Ndipo Shaulo anamwalira, ndipo Baala-Hanani mwana wamwamuna wa Akibori analamulira m'malo mwake. Ndipo Baala-Hanani mwana wamwamuna wa Akibori anamwalira, ndipo Hadari analamulira m'malo mwake; dzina la mudzi wake ndi Pau; ndipo dzina la mkazi wake ndi Mehetabele, mwana wamkazi wa Matiredi, mwana wamkazi wa Mezahabu. Maina a mafumu obadwa kwa Esau, monga mabanja ao, monga malo ao, monga maina ao ndi awa: mfumu Timna, mfumu Aliva, mfumu Yeteti: mfumu Oholibama, mfumu Ela, mfumu Pinoni; mfumu Kenazi, mfumu Temani, mfumu Mibizara; mfumu Magadiele, mfumu Iramu; amenewa ndi mafumu a Edomu, monga mwa kukhala kwao m'dziko lokhala laolao. Uyo ndiye Esau atate wao wa Aedomu. Ndipo Yakobo anakhala m'dziko limene anakhalamo mlendo atate wake, m'dziko la Kanani. Mibadwo ya Yakobo ndi iyi; Yosefe anali wa zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri analinkudyetsa zoweta pamodzi ndi abale ake; ndipo anali mnyamata pamodzi ndi ana a Biliha, ndi ana amuna a Zilipa, akazi a atate wake; ndipo Yosefe anamfotokozera atate wake mbiri yao yoipa. Koma Israele anamkonda Yosefe koposa ana ake onse, pakuti anali mwana wa ukalamba wake; ndipo anamsokera iye malaya amwinjiro. Ndipo abale ake anaona kuti atate wake anamkonda iye koposa abale ake onse: ndipo anamuda iye, ndipo sanathe kulankhula ndi iye mwamtendere. Yosefe ndipo analota loto, nawafotokozera abale ake; ndipo anamuda iye koposa. Ndipo iye anati kwa iwo, Tamvanitu loto limene ndalota: pakuti taonani, ndinalinkumanga mitolo m'munda, ndipo taonani, mtolo wanga unauka nuima chilili! Ndipo taonani, mitolo yanu inadza niuzinga kwete, niuweramira mtolo wanga. Abale ake ndipo anati kwa iye, Kodi udzakhala mfumu yathu ndithu? Kapena udzatilamulira ife ndithu kodi? Ndipo anamuda iye koposa chifukwa cha maloto ake ndi mau ake. Ndipo analotanso loto lina, nafotokozera abale ake, nati, Taonani, ndalotanso loto lina: ndipo taonani, dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi khumi ndi imodzi zinandiweramira ine. Ndipo iye anafotokozera atate wake ndi abale ake; ndipo atate wake anamdzudzula, nati kwa iye, Loto limene walota iwe nlotani? Kodi ine ndi amai ako ndi abale ako tidzafika ndithu tokha kuweramira iwe pansi? Ndipo abale ake anamchitira iye nsanje, koma atate wake anasunga mau amene m'mtima mwake. Ndipo abale ake ananka kukaweta zoweta za atate wao m'Sekemu. Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Kodi abale ako sadyetsa zoweta m'Sekemu? Tiyeni, ndikutuma iwe kwa iwo. Ndipo anati, Ndine pano. Ndipo anati kwa iye, Pita tsopano, nukaone ngati abale ako ali bwino, ndi ngati zoweta zili bwino; nundibwezere ine mau. Ndipo anamtuma iye kuchokera m'chigwa cha Hebroni, ndipo anadza ku Sekemu. Ndipo anampeza munthu, taonani, analinkusokera m'thengo; munthuyo ndipo anamfunsa, nati, Kodi ufuna chiyani? Ndipo iye anati, Ndifuna abale anga. Undiuzetu kumene adyetsa zoweta. Munthuyo ndipo anati, Anachoka pano; pakuti ndinamva alinkuti, Timuke ku Dotani. Yosefe ndipo anatsata abale ake, nawapeza ali ku Dotani. Ndipo iwo anamuona iye ali patali, ndipo asanayandikire pafupi ndi iwo, anampangira iye chiwembu kuti amuphe. Ndipo anati wina ndi mnzake, Taonani, alinkudza mwini maloto uja. Tiyeni tsopano timuphe iye timponye m'dzenje, ndipo tidzati, Wajiwa ndi chilombo; ndipo tidzaona momwe adzachita maloto ake. Ndipo Rubeni anamva nampulumutsa iye m'manja mwao; nati, Tisamuphe iye. Ndipo Rubeni anati kwa iwo, Musakhetse mwazi; mponyeni iye m'dzenjemo m'chipululu muno, koma musamsamulire iye manja: kuti ampulumutse iye m'manja mwao, ambwezenso kwa atate wake. Ndipo panali pamene Yosefe anafika kwa abale ake, anamvula Yosefe malaya ake, malaya amwinjiro amene anavala iye; ndipo anamtenga iye, namponya m'dzenjemo; m'dzenjemo munalibe kanthu, munalibe madzi m'menemo. Ndipo iwo anakhala pansi kuti adye chakudya; ndipo anatukula maso ao, nayang'ana, ndipo taonani, ulendo wa Aismaele anachokera ku Giliyadi ndi ngamira zao, zilinkunyamula zonunkhira ndi mafuta amankhwala ndi mure alinkumuka kutsikira nazo ku Ejipito. Ndipo Yuda anati kwa abale ake, Nanga tidzapindulanji tikamupha mbale wathu ndi kufotsera mwazi wake? Tiyeni timgulitse iye kwa Aismaele, tisasamulire iye manja; chifukwa ndiye mbale wathu, thupi lathu. Ndipo anamvera iye abale ake. Ndipo anapita pamenepo Amidiyani a malonda: ndipo anamtulutsa namkweza Yosefe m'dzenjemo, namgulitsa kwa Aismaele ndi masekeli a siliva makumi awiri; ndipo ananka naye Yosefe ku Ejipito. Ndipo Rubeni anabwera kudzenje, ndipo taonani, Yosefe mulibe m'dzenjemo: ndipo iye anang'amba nsalu yake. Ndipo anabwera kwa abale ake, nati, Mwana palibe; ndipo ine ndipita kuti? Ndipo anatenga malaya ake a Yosefe, napha tonde, naviika malaya m'mwazi wake: natumiza malaya amwinjiro, nadza nao kwa atate ao: ndipo anati, Siwa tawatola; muzindikire tsono ngati ndi malaya a mwana wanu, kapena ndi ena. Ndipo anazindikira nati, Ndiwo malaya a mwana wanga: wajiwa ndi chilombo: Yosefe wakadzulidwa ndithu. Yakobo ndipo anang'amba malaya ake, navala chiguduli m'chuuno mwake namlirira mwana wake masiku ambiri. Ndipo ana amuna ake onse ndi ana akazi onse anauka kuti amtonthoze: koma anakana kutonthozedwa; ndipo anati, Pakuti ndidzatsikira kumanda kwa mwana wanga, ndilinkulirabe. Atate wake ndipo anamlirira. Amidiyani ndipo anamgulitsa iye anke ku Ejipito kwa Potifara, nduna ya Farao, kazembe wa alonda. Ndipo panali nthawi yomweyo, kuti Yuda anatsikira kwa abale ake nalowa kwa Mwadulamu, dzina lake Hira. Ndipo Yuda anaona kumeneko mwana wamkazi wa Mkanani dzina lake Suwa: ndipo anamtenga, nalowa kwa iye. Ndipo anatenga pakati, nabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Eri. Ndipo anatenganso pakati, nabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Onani. Ndipo anabalanso mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Sela: ndipo iye anali pa Kezibu pamene mkazi anambala iye. Ndipo Yuda anamtengera Eri mwana wake woyamba mkazi, ndipo dzina lake ndilo Tamara. Koma Eri mwana wake woyamba wa Yuda anali woipa pamaso pa Yehova: ndipo Yehova anamupha iye. Ndipo Yuda anati kwa Onani, Lowani naye mkazi wa mbale wako, ndi kumchitira mkazi zoyenera mphwake wa mwamuna wake, ndi kumuukitsira mkulu wako mbeu. Ndipo Onani anadziwa kuti mbeu siidzakhala yake: ndipo panali pamene iye analowana naye mkazi wa mbale wake, kuti anaitaya pansi, kuti angampatse mbeu kwa mkulu wake. Koma chimene iye anachita chinali choipa pamaso pa Yehova, ndipo anamupha iyenso. Ndipo Yuda anati kwa Tamara mpongozi wake, Khala wamasiye m'nyumba ya atate wako, kufikira akakula msinkhu Sela mwana wanga wamwamuna: chifukwa anati kuti, Angafe iyenso monga abale ake. Ndipo Tamara ananka nakhala m'nyumba ya atate wake. Atachuluka masiku mwana wamkazi wa Suwa, mkazi wake wa Yuda anafa; ndipo Yuda anatonthola mtima, nakwera kunka kwa akusenga nkhosa zake ku Timna, iye ndi bwenzi lake Hira, Mwadulamu. Ndipo anamuuza Tamara, kuti, Taona, mpongozi wako akwera kunka ku Timna kuti akasenge nkhosa zake. Pamenepo anavula zovala zake zamasiye, nadzifunda ndi chofunda chake, navala nakhala pa chipata cha Enaimu, chifukwa chili pa njira ya ku Timna; pakuti anaona kuti Sela anakula msinkhu, ndipo sanampatse iye kuti akhale mkazi wake. Pamene Yuda anamuona iye, anaganizira kuti ali mkazi wadama: chifukwa iye anabisa nkhope yake. Ndipo iye anapatukira kwa mkazi panjira, nati, Tiyetu, ndilowane nawe; chifukwa sanamdziwe kuti ndiye mpongozi wake. Ndipo anati, Kodi udzandipatsa ine chiyani kuti ulowane ndi ine. Ndipo iye anati, Ndidzatumiza kwa iwe kamwana ka mbuzi ka m'ziweto. Ndipo mkazi nati, Kodi udzandipatsa ine chikole mpaka ukatumiza? Ndipo iye anati, Chikole chanji ndidzakupatsa iwe? Ndipo mkazi anati, Mphete yako, ndi chingwe chako, ndi ndodo ili m'dzanja lako. Ndipo anampatsa izo, nalowana naye, ndipo mkazi anatenga pakati ndi iye. Ndipo mkazi anauka nachoka, navula chofunda chake, navala zovala zamasiye zake. Ndipo Yuda anatumiza kamwana kambuzi ndi dzanja la bwenzi lake Mwadulamu, kuti alandire chikole pa dzanja la mkazi; koma sanampeze iye. Ndipo anafunsa amuna a pamenepo kuti, Ali kuti wadama uja anali pambali pa njira pa Enaimu? Ndipo iwo anati, Panalibe wadama pano. Ndipo iye anabwera kwa Yuda nati, Sitinampeza mkazi; ndiponso amuna a pamenepo anati, Panalibe wadama pano. Ndipo Yuda anati, Azilandire kuti tingachitidwe manyazi: taona, ndinatumiza mwana uyu wa mbuzi, ndipo sunampeza iye. Ndipo panali itapita miyezi itatu, anamuuza Yuda kuti, Tamara mpongozi wako wachita chigololo, ndiponso taonani, ali ndi pakati ndi chigololocho. Ndipo Yuda anati, Mtulutse iye kuti amponye pamoto. Pamene anamtulutsa iye, mkazi anatumiza kwa mpongozi wake kuti, Ndi mwamuna mwini izi ndatenga pakati; ndipo mkazi anati, Tayang'anatu, za yani zimenezi, mphete, ndi chingwe, ndi ndodo? Ndipo Yuda anavomereza nati, Akhale wolungama wopambana ine, chifukwa ine sindinampatsa iye Sela mwana wanga wamwamuna. Ndipo iye sanamdziwenso mkaziyo. Ndipo panali nthawi ya kubala kwake, taonani, amapasa anali m'mimba mwake. Ndipo panali pamene anabala kuti mmodzi anatulutsa dzanja; ndipo namwino anatenga chingwe chofiira namanga pa dzanja lake, kuti, Uyu anayamba kubadwa. Ndipo panali pamene iye anabweza dzanja lake, kuti, taona, mbale wake anabadwa, ndipo namwino anati, Wadziposolera wekha bwanji? Chifukwa chake dzina lake linatchedwa Perezi. Ndipo pambuyo pake anabadwa mbale wake, amene anali ndi chingwe chofiira pamkono pake, dzina lake linatchedwa Zera. Ndipo anatsika naye Yosefe kunka ku Ejipito; ndipo Potifara, nduna ya Farao, kazembe wa alonda, Mwejipito, anamgula iye m'manja mwa Aismaele amene anatsika naye kunka kumeneko. Ndipo Yehova anali ndi Yosefe; ndipo iye anali wolemeralemera; nakhala m'nyumba ya mbuyake Mwejipito. Ndipo mbuyake anaona kuti Yehova anali ndi iye, ndi kuti Yehova anamlemereza m'dzanja lake zonse anazichita. Ndipo Yosefe anapeza ufulu pamaso pake, ndipo anamtumikira iye; ndipo anamuyesa iye woyang'anira pa nyumba yake, naika m'manja mwake zonse anali nazo. Ndipo panali chiyambire anamuyesa iye woyang'anira pa nyumba yake, ndi pa zake zonse, Yehova anadalitsa nyumba ya Mwejipito chifukwa cha Yosefe; ndipo mdalitso wa Yehova unali pa zake zonse, m'nyumba ndi m'munda. Ndipo iye anasiya zake zonse m'manja a Yosefe: osadziwa chomwe anali nacho, koma chakudya chimene anadya. Ndipo Yosefe anali wokoma thupi ndi wokongola. Ndipo panali zitapita izi, kuti mkazi wa mbuyake anamyang'anira maso Yosefe: ndipo mkaziyo anati, Gona ndi ine. Koma iye anakana, nati kwa mkazi wa mbuyake, Taonani, mbuyanga sadziwa chimene chili ndi ine m'nyumbamu, ndipo anaika zake zonse m'manja anga; mulibe wina m'nyumba wamkulu ndine; ndipo sanandikanize ine kanthu, koma iwe, chifukwa kuti uli mkazi wake: nanga ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu? Ndipo pali pakunenanena ndi Yosefe tsiku ndi tsiku, iye sanamvere mkazi kugona naye kapena kukhala naye. Ndipo panali, nthawi yomweyo, iye analowa m'nyumba kuti agwire ntchito yake; ndipo munalibe amuna a m'nyumba m'katimo. Ndipo mkazi anagwira iye chofunda chake, nati, Gona ndi ine; ndipo anasiya chofunda chake m'dzanja lake nathawa, natulukira kubwalo. Ndipo panali pamene mkazi anaona kuti anasiya chofunda chake m'dzanja lake, nathawira kubwalo, anaitana amuna a m'nyumba yake, nanena ndi iwo kuti, Taonani, walowetsa kwa ife Muhebri kuti atiseke ife, analowa kwa ine kugona ndi ine, ndipo ndinafuula ndi mau akulu: ndipo panali pamene iye anamva kuti ndinakweza mau anga ndi kufuula, iye anasiya chofunda chake kwa ine nathawira kubwalo. Ndipo anasunga chofunda chake chikhale ndi iye kufikira atabwera kwao mbuyake. Ndipo ananena kwa iye monga mau awa, anati, Analowa kwa ine kapolo wa Chihebri uja, munabwera naye kwathu, kundipunza ine: ndipo panali pamene ndinakweza mau anga ndi kufuula, iye anasiya chovala chake kwa ine, nathawira kunja. Ndipo panali pamene mbuyake anamva mau a mkazi wake, amene ananena kwa iye, kuti, Choterochi anandichitira ine kapolo wako; kuti iye anapsa mtima. Ndipo mbuyake wa Yosefe anamtenga iye namuika m'kaidi, umo anamangidwa akaidi a mfumu: ndipo iye anali m'mwemo m'kaidimo. Koma Yehova anali ndi Yosefe namchitira iye zokoma, nampatsa ufulu pamaso pa woyang'anira kaidi. Ndipo woyang'anira kaidi anapereka m'manja a Yosefe akaidi onse okhala m'kaidimo, ndipo zonse iwo anazichita m'menemo, iye ndiye wozichita. Woyang'anira m'kaidi sanayang'anire kanthu kalikonse kamene kanali m'manja a Yosefe, chifukwa Yehova anali ndi iye; ndipo zimene anazichita, Yehova anazipindulitsa. Ndipo panali zitapita izi, wopereka chikho wa mfumu ya Aejipito ndi wophika mkate wake anamchimwira mbuye wao mfumu ya Aejipito. Ndipo Farao anakwiyira akulu ake awiriwo wamkulu wa opereka chikho, ndi wamkulu wa ophika mkate. Ndipo anaika iwo asungidwe m'nyumba ya kazembe wa alonda, m'kaidi, umo anamangidwa Yosefe. Ndipo kazembe wa alonda anapereka iwo kwa Yosefe, ndipo iye anawatumikira iwo: ndipo anakhala nthawi mosungidwamo. Ndipo analota maloto onse awiri, yense loto lake, usiku umodzi, yense monga mwa kumasulira kwa loto lake, wopereka chikho ndi wophika mkate wa mfumu ya Aejipito, amene anamangidwa m'kaidi. Ndipo Yosefe analowa kwa iwo m'mawa, nawaona iwo, taonani, anali oziya. Ndipo anafunsa akulu a Farao osungidwa naye m'nyumba ya mbuyake, kuti, Nkhope zanu zagwa bwanji lero? Ndipo iwo anati kwa iye, Ife talota maloto, ndipo tilibe wotimasulira. Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Kodi Mwini kumasulira si ndiye Mulungu? Mundifotokozeretu. Ndipo wopereka chikho wamkulu anafotokozera Yosefe loto lake, nati kwa iye, M'kulota kwanga, taona, mpesa unali pamaso panga: ndipo m'mpesamo munali nthambi zitatu: ndipo unali wonga unaphuka, ndipo maluwa ake anaphuka; nabala matsamvu ake mphesa zakucha; ndipo chikho cha Farao chinali m'dzanja langa: ndipo ndinatenga mphesa, ndi kufinyira m'chikho cha Farao ndi kupereka chikho m'dzanja la Farao. Ndipo Yosefe anati kwa iye, Kumasulira kwake ndi uwu: nthambi zitatu ndizo masiku atatu; akali masiku atatu Farao adzatukula mutu wako, nadzabwezera iwe ntchito yako; ndipo udzapereka chikho cha Farao m'dzanja lake, monga kale lomwe m'mene unali wopereka chikho chake. Koma undikumbukire ine m'mene kudzakhala bwino ndi iwe, ndipo undichitiretu ine kukoma mtima: nunditchule ine kwa Farao, nunditulutse ine m'nyumbamu: chifukwa kuti ndinabedwa ndithu m'dziko la Ahebri; ndiponso pano sindinachite kanthu kakundiikira ine m'dzenjemu. Pamene wophika mkate anaona kuti kumasulira kwake kunali kwabwino, iye anati kwa Yosefe, Inenso ndinalimkulota, ndipo, taonani, malichero atatu a mikate yoyera anali pamtu panga; m'lichero lapamwamba munali mikate ya Farao ya mitundumitundu; ndipo mbalame zinadya ya m'lichero la pamutu panga. Ndipo Yosefe anayankha nati, Kumasulira kwake ndi uku: malichero atatu ndiwo masiku atatu; akali masiku atatu Farao adzakweza mutu wako ndi kuuchotsa, nadzakupachika iwe pamtengo: ndipo mbalame zidzadya mnofu wako. Ndipo panali tsiku lachitatu ndilo tsiku lakubadwa kwake kwa Farao, iye anakonzera anyamata ake madyerero, ndipo anakweza mutu wa wopereka chikho wamkulu ndi mutu wa wophika mkate wamkulu pakati pa anyamata ake. Ndipo anabwezanso wopereka chikho ku ntchito yake; ndipo iye anapereka chikho m'manja a Farao. Koma anampachika wophika mkate wamkulu; monga Yosefe anawamasulira. Koma wopereka chikho wamkulu sanakumbukire Yosefe, koma anamuiwala. Ndipo panali zitapita zaka ziwiri zamphumphu, Farao analota; ndipo, taonani, anaima panyanja. Ndipo, taonani, zinatuluka m'nyanja ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri za maonekedwe okoma ndi zonenepa; ndipo zinadya mabango. Ndipo, taonani ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zinatuluka m'nyanjamo pambuyo pao, za maonekedwe oipa ndi zoonda; ndipo zinaima pa ng'ombe zinazo m'mphete mwa nyanja. Ndipo ng'ombe zazikazi za maonekedwe oipa ndi zoonda zinadya ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri za maonekedwe abwino ndi zonenepazo. Ndipo Farao anauka. Ndipo anagona nalotanso kachiwiri; ndipo taonani, ngala zisanu ndi ziwiri za tirigu zinamera pa mbuwa imodzi, zonenepa ndi zabwino. Ndipo, taonani, ngala zisanu ndi ziwiri, zoonda zopserera ndi mphepo ya kum'mawa, zinamera pambuyo pao. Ndipo ngala zoondazo zinameza ngala zisanu ndi ziwiri zonenepa ndi zodzalazo. Ndipo Farao anauka, ndipo, taonani, analota. Ndipo panali m'mamawa mtima wake unavutidwa; ndipo anatumiza naitana amatsenga onse a m'Ejipito, ndi anzeru onse a momwemo: ndipo Farao anafotokozera iwo loto lake; koma panalibe mmodzi anakhoza kuwamasulira iwo kwa Farao. Pamenepo wopereka chikho wamkulu anati kwa Farao, kuti, Ine ndidzakumbukira zochimwa zanga lero. Farao anakwiya ndi anyamata ake, nandiika ine ndisungidwe m'nyumba ya kazembe wa alonda, ine ndi wophika mkate wamkulu: ndipo tinalota loto usiku umodzi ine ndi iye; tinalota munthu yense monga mwa kumasulira kwa loto lake. Ndipo panali ndi ife mnyamata Muhebri, kapolo wa kazembe wa alonda, ndipo ife tinafotokozera iye, ndipo iye anatimasulira ife maloto athu; kwa munthu yense monga loto lake anatimasulira. Ndipo panali monga momwe iye anatimasulira, momwemo mudachitika; ine anandibwezera mu utumiki wanga, mnzanga anampachika. Ndipo Farao anatumiza nakaitana Yosefe; ndipo anamtulutsa iye msanga m'dzenjemo: ndipo iye anameta, napindula malaya ake, nalowa kwa Farao. Farao ndipo anati kwa Yosefe, Ine ndalota loto, koma palibe wondimasulira; ndipo ndamva alikunena za iwe kuti, ukamva loto udziwa kumasulira. Ndipo Yosefe anayankha Farao kuti, Si mwa ine; koma Mulungu adzayankha Farao mwamtendere. Ndipo Farao ananena kwa Yosefe, M'loto langa taona, ndinaima m'mphepete mwa nyanja; ndipo taona, zinatuluka m'nyanjamo ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri, zonenepa ndi za maonekedwe abwino; ndipo zinadya m'mabango; ndipo taona, ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zina zinatuluka pambuyo pao zosauka ndi za maonekedwe oipa ndi zoonda, zoipa zotere sindinazione m'dziko la Ejipito; ndipo ng'ombe zazikazi zoonda ndi za maonekedwe oipa zinadya ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zonenepa. Ndipo pamene zinadya sizinadziwika kuti zinadya; koma zinaipabe m'maonekedwe ao monga poyamba. Pamenepo ndinauka. Ndipo ndinaona m'kulota kwanga, taona, ngala zisanu ndi ziwiri zinamera pa mbuwa imodzi zodzala ndi zabwino; ndipo, taona, ngala zisanu ndi ziwiri zina zofota, zoonda, zopserera ndi mphepo ya kum'mawa, zinamera pambuyo pao; ndipo ngala zoonda zinameza ngala zisanu ndi ziwiri zabwino; ndipo ndinafotokozera amatsenga: koma panalibe wondimasulira ine. Ndipo Yosefe anati kwa Farao, Loto la Farao lili limodzi: chimene Mulungu ati achite wam'masulira Farao. Ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zabwino ndizo zaka zisanu ndi ziwiri, ndi ngala zisanu ndi ziwiri zabwino ndizo zaka zisanu ndi ziwiri: loto lili limodzi. Ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zoonda ndi za maonekedwe oipa zinatuluka pambuyo pao ndizo zaka zisanu ndi ziwiri, ndiponso ngala zisanu ndi ziwiri zopanda kanthu zopserera ndi mphepo ya kum'mawa, ndizo zaka zisanu ndi ziwiri za njala. Ichi ndi chinthu chimene ndinena kwa Farao: chimene Mulungu ati achite wasonyeza kwa Farao. Taonani, zidzafika zaka zisanu ndi ziwiri zakuchuluka chakudya m'dziko lonse la Ejipito; ndipo pambuyo pao zidzauka zaka zisanu ndi ziwiri za njala; ndipo anthu adzaiwala zochuluka zonsezo m'dziko la Ejipito; ndipo njala idzapululutsa dziko; ndipo zochuluka sizidzazindikirika chifukwa cha njala ikudza m'mbuyoyo, pakuti idzavuta. Ndipo lotolo linabwezedwa kawiri kwa Farao, chifukwa chinthu chili chokhazikika ndi Mulungu, ndipo Mulungu afulumira kuchichita. Tsopano, Farao afunefune munthu wakuzindikira ndi wanzeru, amkhazike iye ayang'anire dziko la Ejipito. Farao achite chotere, alembe woyang'anira dziko wosonkhetsa limodzi la magawo asanu la dziko la Ejipito m'zaka zisanu ndi ziwiri zakuchuluka dzinthu. Iwo asonkhanitse chakudya chonse cha zaka zabwino izo zilinkudzazo, aunjike tirigu m'manja a Farao akhale chakudya m'midzi, namsunge. Ndipo chakudyacho chidzakhala m'dziko chosonkhera zaka zisanu ndi ziwiri za njala imene idzakhala m'dziko la Ejipito; kuti dziko lisaonongedwe ndi njala. Ndipo chinthucho chinali chabwino m'maso mwa Farao, ndi m'maso mwa anyamata ake. Ndipo Farao anati kwa anyamata ake, Kodi ife tidzaone munthu ngati uyu, mzimu wa Mulungu uli m'mtima mwake? Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Popeza Mulungu wakuonetsa iwe zonsezo palibe wina wakuzindikira ndi wanzeru ngati iwe. Uziyang'anira pa nyumba yanga, ndipo anthu anga onse adzalamulidwa mwa mau ako; pa mpando wachifumu pokha ine ndidzakuposa iwe. Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Taona, ndakhazika iwe wolamulira dziko lonse la Ejipito. Ndipo Farao anachotsa mphete yosindikizira yake pa dzanja lake, naiveka pa dzanja la Yosefe, namveka iye ndi zovalira zabafuta, naika unyolo wagolide pakhosi pake; ndipo anamkweza iye m'galeta wake wachiwiri amene anali naye: ndipo anafuula patsogolo pa iye, Gwadani; ndipo anamkhazika iye wolamulira dziko lonse la Ejipito. Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Ine ndine Farao, ndipo popanda iwe palibe munthu aliyense adzatukula dzanja lake kapena mwendo wake m'dziko lonse la Ejipito. Ndipo Farao anamutcha dzina la Yosefe Zafenati-Panea; ndipo anampatsa akwatire Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni. Ndipo Yosefe anatuluka wolamulira, nayendayenda m'dziko la Ejipito. Ndipo Yosefe anali wa zaka makumi atatu pamene iye anaima pamaso pa Farao mfumu ya Aejipito. Ndipo Yosefe anatuluka pamaso pa Farao, napitapita pa dziko lonse la Ejipito. Ndipo zaka zisanu ndi ziwiri zakuchuluka dzinthu nthaka inabala zambirimbiri. Ndipo anasonkhanitsa chakudya chonse cha zaka zisanu ndi ziwiri chimene chinali m'dziko la Ejipito, nasunga chakudyacho m'midzi; chakudya cha m'minda, yozinga midzi yonse, anachisunga m'menemo. Ndipo Yosefe anasunga tirigu ngati mchenga wa panyanja, wambirimbiri kufikira analeka kuwerenga; chifukwa anali wosawerengeka. Ndipo kwa Yosefe anabadwa ana amuna awiri, chisanafike chaka cha njala, amene Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni anambalira iye. Ndipo Yosefe anamutcha dzina la woyamba Manase, chifukwa anati iye, Mulungu wandiiwalitsa ine zovuta zanga zonse, ndi nyumba yonse ya atate wanga. Ndipo dzina la wachiwiri anamutcha Efuremu: chifukwa Mulungu anandibalitsa ine m'dziko la kusauka kwanga. Ndipo zaka zakuchuluka dzinthu zisanu ndi ziwiri za m'dziko la Ejipito, zinatha. Ndipo zinayamba kufika zaka zisanu ndi ziwiri za njala, monga ananena Yosefe; ndipo munali njala m'maiko monse; koma m'dziko lonse la Ejipito munali chakudya. Ndipo pamene dziko lonse la Ejipito linali ndi njala, anthu anafuulira Farao awapatse chakudya; ndipo Farao anati kwa Aejipito onse, Pitani kwa Yosefe: chimene iye anena kwa inu chitani. Ndipo njala inali pa dziko lonse lapansi; ndipo Yosefe anatsegula nkhokwe zonse nagulitsa Aejipito: ndipo njala inakula m'dziko la Ejipito. Ndipo maiko onse anafika ku Ejipito kudzagula tirigu kwa Yosefe: chifukwa njala inakula m'dziko lonse lapansi. Ndipo anaona Yakobo kuti m'Ejipito munali tirigu, nati Yakobo kwa ana ake amuna, Chifukwa chanji mulinkuyang'anana? Ndipo iye anati, Taonani, ndamva kuti m'Ejipito muli tirigu, mutsikireko mutigulire kumeneko; kuti tikhale ndi moyo, tisafe. Ndipo abale ake a Yosefe khumi anatsikira kukagula tirigu m'Ejipito. Koma Yakobo sanamtume Benjamini mphwake wa Yosefe, pamodzi ndi abale ake, chifukwa anati, Choipa chingam'gwere iye. Ndipo ana amuna a Israele anadza kudzagula mwa iwo amene anadzako, pakuti m'dziko la Kanani munali njala. Ndipo Yosefe anali wolamulira dziko; ndiye amene anagulitsa kwa anthu onse a m'dziko; ndipo anafika abale ake a Yosefe, namweramira pansi, nkhope zao pansi. Ndipo Yosefe anaona abale ake, ndipo anazindikira iwo, koma anadziyesetsa kwa iwo ngati mlendo, nanena kwa iwo mwankhanza: ndipo anati kwa iwo, Mufuma kuti inu? Nati iwo, Ku dziko la Kanani kudzagula chakudya. Ndipo Yosefe anazindikira abale ake, koma iwo sanamzindikire iye. Ndipo Yosefe anakumbukira maloto amene analota za iwo, ndipo anati kwa iwo, Ozonda inu; mwadzera kudzaona usiwa wa dziko. Ndipo iwo anati kwa iye, Iai, mbuyanga, koma akapolo anu adzera kudzagula chakudya. Tonse tili ana amuna a munthu mmodzi; tili oona, akapolo anu, sitili ozonda. Ndipo iye anati kwa iwo, Iai, koma mwadzera kuti muone usiwa wa dziko. Nati iwo, Akapolo anu ndife abale khumi, ana amuna a munthu mmodzi m'dziko la Kanani; ndipo, taonani, wamng'ono ali ndi atate wathu lero; ndipo palibe mmodzi. Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Ndicho chimene ndinakunenani inu, kuti, Ndinu ozonda. Mudzayesedwa ndi ichi, pali moyo wa Farao, simudzatuluka muno, koma akadze kuno mphwanu ndiko. Tumizani mmodzi wa inu akatenge, adze naye mphwanu: ndipo inu mudzamangidwa kuti mau anu ayesedwe, ngati zoona zili mwa inu: penatu, pali moyo wa Farao, muli ozonda ndithu. Ndipo anaika onse m'kaidi masiku atatu. Ndipo Yosefe anati kwa iwo tsiku lachitatu, Chitani ichi, kuti mukhale ndi moyo; ine ndiopa Mulungu; ngati muli oona, mmodzi wa abale anu amangidwe m'kaidi momwemo; mukani inu, mupite naye tirigu wa njala ya mabanja anu; koma mukatenge mphwanu kudza naye kwa ine, kuti atsimikizidwe mau anu ndipo simudzafa. Ndipo anachita chomwecho. Ndipo iwo anati wina ndi mnzake, Tachimwiratu mbale wathu, pamene tinaona kuvutidwa kwa mtima wake, potipembedzera ife, koma ife tinakana kumvera, chifukwa chake kuvutidwa kumene kwatifikira. Ndipo Rubeni anayankha nati kwa iwo, Kodi sindinanena kwa inu kuti, Musachimwire mwanayu; ndipo inu munakana kumvera? Chifukwa chakenso, taonani mwazi wake ufunidwa. Ndipo sanadziwe kuti Yosefe anamva; chifukwa anali ndi womasulira. Ndipo anawafotokozera iwo nalira, nawatembenukiranso, nanena nao, nampatula Simeoni mwa iwo, nammanga iye pamaso pao. Ndipo Yosefe analamulira kuti adzaze zotengera zao ndi tirigu, ndi kubweza ndalama zao, aliyense m'thumba mwake, ndi kuwapatsa phoso la panjira; ndipo anatero nao. Ndipo anasenzetsa abulu ao tirigu wao nachokapo. Ndipo pamene wina wa iwo anamasula thumba lake kuti adyetse bulu wake pachigono, anapeza ndalama zake; taonani, zinali kukamwa kwa thumba lake. Ndipo iye anati kwa abale ake, Wandibwezera ine ndalama zanga, taonani, zili kukamwa kwa thumba langa; ndipo mitima yao inawadera iwo, nanthunthumira, natembenukirana wina ndi mnzake kuti, Nchiyani ichi Mulungu watichitira ife? Ndipo anadza kwa Yakobo atate wao ku dziko la Kanani, namfotokozera iye zonse zinaonekera kwa iwo; kuti, Munthu mwini dziko, ananena ndi ife mwankhalwe, natiyesa ife ozonda dziko. Koma ife tinati kwa iye, Tili anthu oona; sitili ozonda; tili abale khumi ndi awiri, ana a atate wathu; wina palibe, ndipo lero wamng'ono ali ndi atate wathu m'dziko la Kanani. Ndipo munthuyo mwini dziko anati kwa ife, Momwemu ndidzadziwa kuti muli anthu oona; siyani mmodzi wa abale anu pamodzi ndi ine, tengani tirigu wa njala ya kwanu, mukani; idzani naye mphwanu kwa ine, ndipo ndidzadziwa kuti simuli ozonda koma anthu oona: chomwecho ndidzakubwezerani inu mbale wanu, ndipo mudzachita malonda m'dziko muno. Ndipo panali pamene analikukhuthula matumba ao, taonani, phukusi la ndalama la yense linali m'thumba lake; ndipo pamene iwo ndi atate ao anaona mapukusi a ndalama anaopa. Ndipo Yakobo atate wao anati kwa iwo, Munandilanda ine ana; Yosefe palibe, Simeoni palibe, ndipo mudzachotsa Benjamini: zonse zimene zandigwera. Ndipo Rubeni anati kwa atate wake, kuti, Muwaphe ana anga amuna awiri ndikapanda kumbweza iye kwa inu; mumpereke iye m'manja mwanga, ndipo ine ndidzambwezanso kwa inu. Ndipo iye anati, Mwana wanga sadzatsikira ndi inu, chifukwa kuti mkulu wake wafa, ndipo watsala iye yekha; ngati choipa chikamgwera iye m'njira m'mene mupitamo, inu mudzatsitsira ndi chisoni imvi zanga kumanda. Ndipo njala inakula m'dzikomo. Ndipo panali pamene atatha kudya tirigu yense anatengayo ku Ejipito atate wao anati kwa iwo, Pitaninso, mukatigulire ife chakudya pang'ono. Ndipo Yuda ananena ndi iye kuti, Munthu uja anatilimbitsira mau kuti, simudzaonanso nkhope yanga, koma mphwanu akhale ndi inu ndiko. Ngati mudzatuma mphwathu pamodzi ndi ife, tidzatsikira ndi kugulira inu chakudya. Koma mukapanda kumtuma iye sititsika; pakuti munthu uja anati kwa ife, Simudzaona nkhope yanga, ngati mphwanu sali ndi inu. Ndipo Israele anati, Chifukwa ninji munandichitira ine choipa chotero kuti munamuuza munthuyo muli ndi mphwanu? Ndipo iwo anati, Munthuyo anafunsitsa za ife, ndi za abale athu, kuti, Atate wanu alipo? Kodi muli ndi mphwanu? Ndipo tinamfotokozera iye monga mwa mau amenewo: ngati tinadziwa kuti iye adzati, Idzani naye mphwanu? Ndipo Yuda anati kwa atate wake Israele, Mumtume mnyamata pamodzi ndi ine ndipo ife tidzanyamuka ndi kupita; kuti tikhale ndi moyo tisafe, ife ndi inu ndi ana athu ang'ono. Ine ndidzakhala chikole, pa manja anga mudzamfunsa: ndikapanda kumbwezera kwa inu ndi kumuimitsa pamaso panu, chifukwa chake chidzakhala pa ine masiku onse: pakuti tikadaleka kuchedwa mwenzi tsopano titabwera kawiri. Ndipo Israele atate wao anati kwa iwo, Ngati chomwecho tsopano chitani ichi: tengani zipatso za m'dziko muno m'zotengera zanu, mumtengere munthu uja mphatso, mafuta amankhwala pang'ono, ndi uchi pang'ono, zonunkhira ndi mure, ndi mfula, ndi katungurume; nimutenge ndalama zowirikiza m'manja mwanu; ndipo ndalama zimene zinabwezedwa kukamwa kwa matumba anu mutengenso m'manja mwanu; kapena sanachite dala; mutengenso mphwanu, nimunyamuke, mupitenso kwa munthu uja: Mulungu Wamphamvuyonse adzakupatsani inu chifundo pamaso pa munthu uja, kuti akumasulireni inu mbale wanu wina ndi Benjamini. Ndipo ine, ngati ndikhala wopanda ana, ndikhalatu. Amunawo ndipo anatenga mphatso natenga ndalama zowirikiza m'manja mwao, ndi Benjamini; ndipo ananyamuka ndi kutsikira ku Ejipito, naima pamaso pa Yosefe. Ndipo pamene Yosefe anaona Benjamini pamodzi nao, anati kwa tsanyumba wake, Lowa nao anthuwo m'nyumba, kaphere iwo, kakonzere, chifukwa anthuwo adzadya ndi ine usana uno. Munthuyo anachita monga anamuuza Yosefe, ndipo munthuyo analowa nao anthuwo m'nyumba ya Yosefe. Anthuwo ndipo anaopa, chifukwa analowezedwa m'nyumba ya Yosefe; nati, Chifukwa cha ndalama zija zinabwezedwa m'matumba athu nthawi yoyamba ija, ife tilowezedwa, kuti aone chifukwa ndi ife, atigwere ife, atiyese ife akapolo, ndi abulu athu. Ndipo anayandikira kwa tsanyumba wa Yosefe, ndipo ananena ndi iye pa khomo la nyumba, nati, Mfumu, tinatsikira ndithu nthawi yoyamba kudzagula chakudya: ndipo panali pamene ife tinafika pachigono, tinamasula matumba athu, ndipo taonani ndalama za yense zinali kukamwa kwa thumba lake, ndalama zathu mkulemera kwake; ndipo tabwera nazo m'manja mwathu. Ndalama zina tatenga m'manja mwathu kuti tigule chakudya: sitimdziwa amene anaika ndalama zathu m'matumba athu. Ndipo iye anati, Mtendere ukhale ndi inu, musaope; Mulungu wanu ndi Mulungu wa atate wanu anakupatsani inu chuma m'matumba anu; ine ndinali nazo ndalama zanu. Pamenepo anawatulutsira Simeoni. Ndipo munthuyo analowetsa anthu m'nyumba ya Yosefe, nawapatsa iwo madzi, natsuka mapazi ao, napatsa abulu ao chakudya. Ndipo anakonzeratu mphatso asanafike Yosefe usana; chifukwa anamva kuti adzadya chakudya pamenepo. Pamene Yosefe anadza kunyumba kwake, analowa nazo m'nyumba mphatso zinali m'manja mwao, namweramira iye pansi. Ndipo anafunsa iwo za ubwino wao, nati, Kodi atate wanu ali ndi moyo? Wokalamba uja amene munanena uja: kodi alipo? Ndipo iwo anati, Kapolo wanu atate wathu ali bwino, alipo. Ndipo anawerama, namgwadira iye. Ndipo iye anatukula maso ake naona Benjamini mphwake, mwana wa amake, nati, Kodi uyu ndi mphwanu wamng'ono uja, amene munanena ndi ine uja? Ndipo iye anati, Mulungu akuchitire iwe ufulu, mwana wanga. Yosefe ndipo anafulumira, chifukwa mtima wake unakhumbitsa mphwake, ndipo anafuna polirira; nalowa m'chipinda chake naliramo. Ndipo anasamba nkhope yake, natuluka; ndipo anadziletsa, nati, Ikani chakudya. Ndipo anamuikira iye chake pa yekha, ndi iwo chao pa okha, ndi Aejipito akudya naye chao pa okha; chifukwa Aejipito sanathei kudya chakudya pamodzi ndi Ahebri: chifukwa kuchita chomwecho nkunyansira Aejipito. Ndipo anakhala pamaso pake, woyamba monga ukulu wake, ndi wamng'ono monga ung'ono wake; ndipo anazizwa wina ndi wina. Ndipo anawagawira mitanda ya patsogolo pake; koma mtanda wa Benjamini unaposa mitanda ya onsewo kasanu. Ndipo anamwa, nasekera pamodzi ndi iye. Ndipo Yosefe anauza tsanyumba wake kuti, Dzaza matumba a anthuwo ndi chakudya, monga angathe kunyamula, ndi kuika ndalama za yense kukamwa kwa thumba lake. Nuike chikho changa, chikho chasiliva chija, kukamwa kwa thumba la wamng'ono, pamodzi ndi ndalama za tirigu zake. Ndipo iye anachita monga mau ananena Yosefe. Pamene kudacha, anamukitsa anthu iwo ndi abulu ao. Atatuluka m'mudzi asanamuke patali, Yosefe anati kwa tsanyumba wake, Tanyamuka, talondola anthu aja, ukawapeza unene nao, Chifukwa chanji mwabwezera zoipa m'malo mwa zabwino? Kodi si ndicho chomwera nacho mbuyanga, naombeza ula nacho? Mwachitira choipa pakutero. Ndipo anapeza iwo, nanena nao mau omwewo. Nati kwa iye, Bwanji mbuyanga anena mau otere? Ngati nkutheka kuti akapolo anu achite chotero? Taonani, ndalama zija, tinazipeza kukamwa kwa matumba athu, tinazibwezanso kwa inu kutuluka m'dziko la Kanani; nanga bwanji tingabe m'nyumba ya mbuyanga kapena siliva kapena golide? Iye wa akapolo anu ampeza nacho afe, ndipo ifenso tidzakhala akapolo a mbuyanga. Ndipo iye anati, Tsononso chikhale monga mwa mau anu: iye amene ampeza nacho adzakhala kapolo wanga; ndipo inu mudzakhala opanda chifukwa. Ndipo anafulumira natsitsa pansi yense thumba lake, namasula yense thumba lake. Ndipo iye anafunafuna kuyambira pa wamkulu naleka pa wamng'ono nachipeza chikho m'thumba la Benjamini: ndipo anang'amba zovala zao, nasenzetsa yense bulu wake, nabwera kumudzi. Yudanso ndi abale ake anadza kunyumba ya Yosefe; ndipo iye akali pamenepo; ndipo anagwa pansi patsogolo pake. Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Ichi nchiyani mwachichita? Kodi simudziwa kuti munthu ngati ine ndingathe kuzindikira ndithu? Ndipo Yuda anati, Kodi tidzati bwanji kwa mbuyanga? Kodi tidzanenanji? Kapena tidzawiringula ife bwanji? Mulungu wapeza mphulupulu ya akapolo anu; taonani, tili akapolo a mbuyanga, ife ndi iye amene anampeza nacho chikho m'dzanja lake. Ndipo iye anati, Ngati kutheka kuti ndichite chotero! Munthu amene anampeza nacho m'dzanja lake adzakhala kapolo wanga: koma inu, kazipitani ndi mtendere kwa atate wanu. Ndipo Yuda anayandikira kwa iye nati, Mfumu, kapolo wanu aneneretu m'makutu a mbuyanga, mtima wanu usapse pokwiya ndi kapolo wanu; chifukwa muli ngati Farao. Mbuyanga anafunsa akapolo ake kuti, Kodi muli ndi atate wanu kapena mbale wanu? Ndipo tinati kwa mbuyanga, Tili ndi atate, munthu wokalamba, ndi mwana wa ukalamba wake wamng'ono; mbale wake wafa, ndipo iye yekha watsala wa amake, ndipo atate wake amkonda iye. Ndipo munati kwa akapolo anu, Munditengere iye, kuti ndimuone iye m'maso mwanga. Ndipo ife tinati kwa mbuyanga, Mnyamata sangathei kumsiya atate wake; pakuti akamsiya atate wake, atate wake adzafa. Ndipo munati kwa akapolo anu, Koma ngati mbale wanu safika pamodzi ndi inu, simudzaonanso konse nkhope yanga. Ndipo panali titakwera kunka kwa kapolo wanu atate wanga, tinamfotokozera iye mau a mbuyanga. Ndipo atate wathu anati, Mupitenso mutigulire ife chakudya pang'ono. Ndipo ife tinati, Sitingathe kupita; mphwathu wamng'ono akakhala ndi ife, pamenepo tidzapita; pakuti sitingaone nkhope ya munthu uja, mphwathu wamng'ono akapanda kukhala ndi ife. Ndipo kapolo wanu atate wanga anati kwa ife, Inu mudziwa kuti mkazi wanga anandibalira ine ana amuna awiri; wina anatuluka kwa ine ndipo ndinati, Zoonatu, wakadzulidwa; ndipo sindidzamuonanso iye; ndipo ngati mukandichotsera ameneyonso, ndipo ngati chimgwera choipa, mudzanditsitsira ndi chisoni imvi zanga kumanda. Chifukwa chake ndikafika kwa kapolo wanu atate wanga, ndipo mnyamata akapanda kukhala ndi ife; popeza moyo wanu uli womangidwa ndi moyo wa mnyamatayo; kudzakhala pakuona kuti mnyamatayo palibe, adzafa; ndipo akapolo anu adzamtsitsira ndi chisoni imvi za atate wathu kumanda. Pakuti kapolo wanu anadziyesa chikole cha mnyamata pa atate wanga, kuti, Ndikapanda kumbwezeranso kwa inu, pamenepo ndidzakhala ndi chifukwa kwa atate wanga nthawi zonse. Tsopanotu, mtumiki wanu akhale kapolo wa mbuyanga m'malo mwa mnyamata; mnyamatayo akwere pamodzi ndi abale ake. Pakuti ndidzakwera bwanji kwa atate wanga, mnyamatayo akapanda kukhala ndi ine? Ndingaone choipa chidzagwera atate wanga. Ndipo Yosefe sanakhoze kudziletsa pamaso pa onse amene anaima naye: nati, Tulutsa anthu onse pamaso panga. Ndipo panalibe munthu pamodzi ndi iye pamene Yosefe anadziululira yekha kwa abale ake. Ndipo analira momveka, ndipo anamva Aejipito, ndipo anamva a m'nyumba ya Farao. Ndipo Yosefe anati kwa abale ake, Ine ndine Yosefe; kodi akali ndi moyo atate wanga? Ndipo abale ake sanakhoze kumyankha iye; pakuti anavutidwa pakumuona iye. Ndipo Yosefe anati kwa abale ake, Muyandikiretu kwa ine; nayandikira. Ndipo iye anati, Ine ndine Yosefe mbale wanu, ine ndemwe munandigulitsa ndilowe m'Ejipito. Tsopano musapwetekwe mtima, musadzikwiyira inu nokha, kuti munandigulitsa ine kuno, pakuti Mulungu ananditumiza ine patsogolo panu kuti ndisunge moyo. Zaka ziwirizi muli njala m'dziko muno; ndipo zatsala zaka zisanu, zopanda kulima kapena kusenga. Ndipo Mulungu anatumiza ine patsogolo panu kuti ndikhazike inu mutsale m'dziko lapansi, ndi kusunga inu amoyo ndi chipulumutso chachikulu. Ndipo tsopano sindinu amene munanditumiza ine ndifike kuno, koma Mulungu, ndipo anandiyesa ine atate wa Farao, ndi mwini banja lake lonse, ndi wolamulira dziko lonse la Ejipito. Fulumirani. Kwerani kunka kwa atate wanga, muti kwa iye, Chotere ati Yosefe mwana wanu, Mulungu wandiyesa ine mwini Ejipito lonse: tsikirani kwa ine, musachedwe. Ndipo mudzakhala m'dziko la Goseni, mudzakhala pafupi ndi ine, inu ndi ana anu, ndi ana a ana anu, ndi nkhosa zanu, ndi zoweta zanu, ndi zonse muli nazo; ndipo ndidzachereza inu komweko; pakuti zatsala zaka zisanu za njala; kuti mungafikire umphawi, inu ndi banja lanu, ndi onse muli nao. Taonani, maso anu aona, ndi maso a mphwanga Benjamini, kuti ndi m'kamwa mwanga ndilikulankhula ndi inu. Ndipo mudzafotokozera atate wanga za ulemerero wanga wonse m'Ejipito, ndi zonse mwaziona; ndipo muzifulumira ndi kutsitsira kuno atate wanga. Ndipo anagwa pakhosi pake pa Benjamini, nalira; ndipo Benjamini nalira pakhosi pake. Ndipo anampsompsona abale ake onse, nalirira iwo; ndipo pambuyo pake abale ake onse anacheza naye. Ndipo mbiri yake inamveka m'nyumba ya Farao, kuti abale ake a Yosefe afika; ndipo inamkomera Farao, ndi anyamata ake. Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Nena ndi abale ako, Chitani ichi; senzetsani nyama zanu, ndi kupita kunka ku dziko la Kanani; katengeni atate wanu ndi mabanja anu, nimudze kwa ine; ndipo ndidzakupatsani inu zabwino za dziko la Ejipito, ndipo mudzadya zonenepa za dzikoli. Tsopano mwalamulidwa chitani ichi; muwatengere ana anu ndi akazi magaleta a m'dziko la Ejipito; nimubwere naye atate wanu. Musasamalire chuma chanu; popeza zabwino za dziko lonse la Ejipito ndi zanu. Ndipo ana a Israele anachita chotero: ndipo Yosefe anawapatsa iwo magaleta monga analamulira Farao, nawapatsa phoso la panjira. Onse anawapatsa yense zovala zopindula; koma Benjamini anampatsa masekeli a siliva mazana atatu ndi zovala zopindula zisanu. Kwa atate wake anatumiza zotere: abulu khumi osenza zinthu zabwino za m'Ejipito, ndi abulu akazi khumi osenza tirigu, ndi chakudya, ndi phoso la atate la panjira. Ndipo anamukitsa abale ake, ndipo anachoka; ndipo anati kwa iwo, Musakangane panjira. Ndipo anakwera kutuluka m'Ejipito, nafika ku dziko la Kanani kwa Yakobo atate wao. Ndipo anamfotokozera iye kuti, Yosefe akali ndi moyo, ndipo alamulira m'dziko lonse la Ejipito. Pamenepo mtima wake unakomoka, pakuti sanawakhulupirire iwo. Ndipo anamfotokozera iye mau onse a Yosefe amene ananena ndi iwo; ndipo pamene anaona magaleta amene Yosefe anatumiza kuti amtengeremo, mtima wa Yakobo atate wao unatsitsimuka; ndipo Israele anati, Chakwana; Yosefe mwana wanga akali ndi moyo; ndidzamuka ndikamuone iye ndisanafe. Ndipo Israele anamuka ulendo wake ndi zonse anali nazo, nafika ku Beereseba, napereka nsembe kwa Mulungu wa Isaki atate wake. Ndipo Mulungu ananena kwa Israele, m'masomphenya a usiku, nati, Yakobo, Yakobo. Nati iye, Ndine pano. Ndipo anati, Ine ndine Mulungu, Mulungu wa atate wako; usaope kunka ku Ejipito; pakuti pamenepo ndidzakusandutsa iwe mtundu waukulu; Ine ndidzatsikira pamodzi ndi iwe ku Ejipito; ndipo Ine ndidzakubwezanso ndithu; ndipo Yosefe adzaika dzanja lake pamaso pako. Ndipo Yakobo anachoka ku Beereseba, ndipo ana amuna a Israele anamnyamula Yakobo atate wao, ndi ana ao ang'ono, ndi akazi ao, m'magaleta amene Farao anatumiza kuti amnyamule iye. Ndipo anatenga ng'ombe zao ndi chuma chao anachipeza m'dziko la Kanani, nadza ku Ejipito, Yakobo ndi mbeu zake zonse pamodzi ndi iye; ana ake amuna, ndi zidzukulu zake zazimuna, ndi ana akazi ake, ndi zidzukulu zake zazikazi, ndi mbeu zake zonse anadza nazo m'Ejipito. Maina a ana a Israele amene anadza m'Ejipito ndi awa: Yakobo ndi ana amuna ake: Rubeni mwana wamwamuna woyamba wa Yakobo. Ndi ana amuna a Rubeni: Hanoki, ndi Palu, ndi Hezironi, ndi Karimi. Ndi ana amuna a Simeoni: Yemuwele ndi Yamini, ndi Ohadi, ndi Yakini, ndi Zohari, ndi Shaulo, mwana wamwamuna wa mkazi wa ku Kanani. Ndi ana amuna a Levi: Geresoni, Kohati, ndi Merari. Ndi ana amuna a Yuda: Eri, ndi Onani, ndi Sela, ndi Perezi, ndi Zera; koma Eri ndi Onani anafa m'dziko la Kanani. Ndi ana amuna a Perezi ndiwo Hezironi ndi Hamuli. Ndi ana amuna a Isakara: Tola ndi Puva, ndi Iyobu, ndi Simironi. Ndi ana amuna a Zebuloni: Seredi, ndi Eloni ndi Yaleele. Amenewo ndi ana amuna a Leya, amene anambalira Yakobo m'Padanaramu, pamodzi ndi mwana wamkazi wake Dina; ana aamuna ndi aakazi onse ndiwo anthu makumi atatu kudza atatu. Ndi ana amuna a Gadi: Zifiyoni, ndi Hagi, ndi Suni, ndi Eziboni, ndi Eri, ndi Arodi, ndi Areli. Ndi ana amuna a Asere: Imina, ndi Isiva, ndi Isivi, ndi Beriya, ndi Sera mlongo wao; ndi ana a Beriya: Hebere, ndi Malikiele. Amenewa ndi ana a Zilipa, amene Labani anampatsa Leya mwana wake wamkazi, amenewo anambalira Yakobo, anthu khumi ndi asanu ndi mmodzi. Ana a Rakele mkazi wake wa Yakobo: Yosefe ndi Benjamini. Kwa Yosefe kunabadwa m'dziko la Ejipito Manase ndi Efuremu, amene Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni anambalira iye. Ndi ana amuna a Benjamini: Bela ndi Bekere, ndi Asibele, ndi Gera, ndi Naamani, ndi Ehi ndi Rosi, Mupimu ndi Hupimu, ndi Aridi. Amenewo ndi ana a Rakele, amene anabadwira Yakobo; anthu onse ndiwo khumi ndi anai. Ndi ana amuna a Dani: Husimu. Ndi ana amuna a Nafutali: Yazeele, ndi Guni, ndi Yezere ndi Silemu Amenewa ndi ana a Biliha, amene Labani anampatsa Rakele mwana wake wamkazi, amenewo anambalira Yakobo; anthu onse ndiwo asanu ndi awiri. Ndi anthu onse amene anadza ndi Yakobo m'Ejipito, amene anatuluka m'chuuno mwake, pamodzi ndi akazi a ana amuna a Yakobo ndiwo makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi mmodzi; ndi ana amuna a Yosefe, amene anambadwira iye m'Ejipito ndiwo anthu awiri; anthu onse a mbumba ya Yakobo, amene analowa m'Ejipito anali makumi asanu ndi awiri. Ndipo anatumiza Yuda patsogolo pake kwa Yosefe, amtsogolere kumuonetsa njira yonka ku Goseni: ndipo anafika ku dziko la Goseni. Ndipo Yosefe anamanga galeta lake nakwera kunka kukakomana naye Israele atate wake, ku Goseni, ndipo anadzionetsera yekha kwa iye, nagwera pakhosi pake nakhala m'kulira pakhosi pake. Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Ndife tsopano, popeza ndaona nkhope yako, kuti ukali ndi moyo. Ndipo Yosefe anati kwa abale ake, ndi kwa mbumba ya atate wake, Ndidzanka, ndikauze Farao, ndipo ndidzati kwa iye, Abale anga ndi mbumba ya atate wanga, amene anali m'dziko la Kanani, afika kwa ine; ndipo anthuwo ali abusa chifukwa anakhala oweta ng'ombe; ndipo anadza ndi nkhosa zao ndi ng'ombe zao ndi zonse ali nazo. Ndipo padzakhala pamene Farao adzaitana inu, nadzati, Ntchito yanu njotani? Mudzati, Akapolo anu akhala oweta ng'ombe chiyambire ubwana wathu kufikira tsopano, ife ndi atate athu; kuti mukhale m'dziko la Goseni; chifukwa abusa onse anyansira Aejipito. Ndipo Yosefe analowa nauza Farao nati, Atate wanga ndi abale anga, ndi nkhosa zao ndi ng'ombe zao, ndi zonse ali nazo, anachokera ku dziko la Kanani; ndipo, taonani, ali m'dziko la Goseni. Ndipo mwa abale ake anatengako anthu asanu, nawaonetsa iwo kwa Farao. Ndipo Farao anati kwa abale ake, Ntchito yanu njotani? Ndipo iwo anati kwa Farao, Akapolo anu ndi abusa, ife ndi atate athu. Nati kwa Farao, Tafika kuti tikhale m'dzikomo; popeza palibe podyetsa zoweta za akapolo anu; pakuti njala yakula m'dziko la Kanani. Mulole tsopano akapolo anu akhale m'dziko la Goseni. Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Atate wako ndi abale ako afika kwa iwe; dziko la Ejipito lili pamaso pako: uwakhazike atate wako ndi abale ako pa dera lokometsetsa la dziko; akhale m'dziko la Goseni; ndipo ngati udziwa anthu anzeru a mwa iwo, uwaike iwo ayang'anire ng'ombe zanga. Ndipo Yosefe analowa naye Yakobo atate wake, namuika iye pamaso pa Farao; ndipo Yakobo anamdalitsa Farao. Ndipo Farao anati kwa Yakobo, Masiku a zaka za moyo wanu ndi angati? Ndipo Yakobo anati kwa Farao, Masiku a zaka za ulendo wanga ndi zaka zana limodzi kudza makumi atatu; masiku a zaka za moyo wanga ali owerengeka ndi oipa, sanafikire masiku a zaka za moyo wa makolo anga m'masiku a ulendo wao. Ndipo Yakobo anamdalitsa Farao, natuluka pamaso pa Farao. Ndipo Yosefe anakhazika atate wake ndi abale ake, napatsa iwo pokhala m'dziko la Ejipito, m'dera lokometsetsa la m'dziko, m'dziko la Ramsesi, monga analamulira Farao. Ndipo Yosefe anachereza atate wake ndi abale ake, ndi mbumba yonse ya atate wake ndi chakudya monga mwa mabanja ao. Ndipo munalibe chakudya m'dziko lonse; pakuti njala inalimba kwambiri; chifukwa chake dziko la Ejipito ndi dziko la Kanani tinalefuka chifukwa cha njalayo. Ndipo Yosefe anasonkhanitsa ndalama zonse anazipeza m'dziko la Ejipito ndi m'dziko la Kanani, za tirigu amene anagula; ndipo Yosefe anapereka ndalama kunyumba ya Farao. Ndipo zitatha ndalama zonse m'dziko la Ejipito ndi m'dziko la Kanani, Aejipito onse anadza kwa Yosefe, nati, Mutipatse ife chakudya; tiferenji pamaso panu? Zatsirizika ndalama. Ndipo Yosefe anati, Mundipatse ng'ombe zanu: ndipo ndidzakupatsani inu mtengo wa ng'ombe zanu ngati ndalama zatsirizika. Ndipo anadza nazo ng'ombe zao kwa Yosefe, ndipo Yosefe anapatsa iwo chakudya chosinthana ndi akavalo, ndi nkhosa ndi ng'ombe ndi abulu; ndipo anawadyetsa iwo ndi chakudya chosinthana ndi zoweta zao zonse chaka chimenecho. Chitatha chaka chimenecho, anadza kwa iye chaka chachiwiri, nati kwa iye, Sitibisira mbuyathu kuti ndalama zathu zonse zatha; ndipo zoweta za ng'ombe nza mbuyathu: palibe kanthu kotsala pamaso pa mbuyathu, koma matupi athu ndi maiko athu; tiferenji pamaso panu, ife ndi dziko lathu? Mutigule ife ndi dziko lathu ndi chakudya, ndipo ife ndi dziko lathu tidzakhala akapolo a Farao; ndipo mutipatse ife mbeu, kuti tikhale ndi moyo, tisafe, ndi kuti dziko lisakhale labwinja. Ndipo Yosefe anamgulira Farao dziko lonse la Ejipito, chifukwa Aejipito anagulitsa yense munda wake, chifukwa njala inakula pa iwo; ndipo dziko linakhala la Farao. Tsono anthu, anasunthira iwo kumidzi kuchokera kumphepete kwa malire a Ejipito kufikira kumphepete kwina kwake. Koma dziko la ansembe lokha sanagule, chifukwa ansembe analandira gawo lao kwa Farao, nadya gawolo anawapatsa Farao; chifukwa chake sanagulitse dziko lao. Ndipo Yosefe anati kwa anthu, Taonani, ndamgulira Farao inu ndi dziko lanu lero lomwe, taonani, mbeu zanu siizi, mubzale m'dziko. Ndipo padzakhala pakukunkha, muzipatsa limodzi la mwa magawo asanu kwa Farao, koma magawo anai ndi anu, mbeu za munda, ndi za chakudya chanu, ndi cha ana anu ndi mabanja anu. Ndipo iwo anati, Watipulumutsa miyoyo yathu; tipeze ufulu pamaso pa mbuyanga, ndipo tidzakhala akapolo a Farao. Ndipo Yosefe analamulira lamulo la pa dziko la Ejipito kufikira lero, kuti Farao alandire limodzi la mwa magawo asanu; koma dziko la ansembe lokha silinakhala la Farao. Ndipo Israele anakhala m'dziko la Ejipito, m'dziko la Goseni; nakhala nazo zaozao m'menemo, nabalana nachuluka kwambiri. Ndipo Yakobo anakhala m'dziko la Ejipito zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri; ndipo masiku a Yakobo zaka za moyo wake zinali zaka zana limodzi mphambu makumi anai kudza zisanu ndi ziwiri. Ndipo nthawi inayandikira kuti Israele adzafa, ndipo anaitana Yosefe mwana wake wamwamuna, nati kwa iye, Ngati ndapeza ufulu pamaso pako, ikatu dzanja lako pansi pa ntchafu yanga, nundichitire ine zabwino ndi zoona: usandiikatu ine m'Ejipito; koma pamene ndidzagona ndi makolo anga, udzanditenge ine kutuluka m'dziko la Ejipito, ukandiike ine m'manda mwao. Ndipo iye anati, Ndidzachita monga mwanena. Ndipo anati, Undilumbirire ine; namlumbirira iye. Ndipo Israele anawerama kumutu kwa kama. Ndipo panali zitapita izi, anthu anati kwa Yosefe, Taonani, atate wanu wadwala: ndipo iye anatenga ana ake amuna awiri, Manase ndi Efuremu, apite naye. Ndipo anthu anamuuza Yakobo nati, Taonani, mwana wanu Yosefe alinkudza kwa inu; ndipo Israele anadzilimbitsa nakhala tsonga pakama. Ndipo Yakobo anati kwa Yosefe, Mulungu Wamphamvuyonse anaonekera kwa ine pa Luzi m'dziko la Kanani nandidalitsa ine, nati kwa ine, Taona, ndidzakubalitsa iwe, ndidzakuchulukitsa iwe, ndidzakusandutsa iwe khamu la anthu a mitundu; ndipo ndidzapatsa mbeu yako ya pambuyo pako dziko ili likhale laolao chikhalire. Tsopano ana ako amuna awiri, amene anakubadwira iwe m'dziko la Ejipito, ndisanadze kwa iwe ku Ejipito, ndiwo anga; Efuremu ndi Manase, monga Rubeni ndi Simeoni, ndiwo anga. Koma obala iwe udzawabala pambuyo pao, ndiwo ako; awatche dzina la abale ao m'cholowa chao. Tsono ine, pamene ndinachokera ku Padani, Rakele anamwalira pambali panga m'dziko la Kanani m'njira, itatsala nthawi yaing'ono tisadafike ku Efurata; ndipo ndidamuika iye pamenepo pa njira ya ku Efurata (ndiwo Betelehemu). Ndipo Israele anayang'ana ana amuna a Yosefe, nati, Ndani awa? Ndipo Yosefe anati kwa atate wake, Amenewa ndi ana anga, amene Mulungu wandipatsa ine pano. Ndipo iye anati, Udze naotu kwa ine, ndipo ndidzawadalitsa. Koma maso a Israele anali akhungu m'ukalamba wake, ndipo sanathei kuona. Ndipo anadza nao pafupi; ndipo anapsompsona iwo, nawafungatira. Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Sindinaganizira kuti ndione nkhope yako: ndipo, taona, Mulungu wandionetsa ine mbeu zako zomwe. Ndipo Yosefe anatulutsa iwo pakati pa maondo ake, nawerama ndi nkhope yake pansi. Ndipo Yosefe anatenga iwo onse awiri, Efuremu m'dzanja lake lamanja ku dzanja lamanzere la Yakobo, ndi Manase m'dzanja lake lamanzere ku dzanja lamanja la Israele, nadza nao pafupi ndi iye. Ndipo Israele anatambalitsa dzanja lake lamanja, naliika pa mutu wa Efuremu, amene ndiye wamng'ono, ndi dzanja lake lamanzere pa mutu wa Manase, anapingasitsa manja ake dala; chifukwa Manase anali woyamba. Ndipo anadalitsa Yosefe, nati, Mulungu, pamaso pake anayenda makolo anga Abrahamu ndi Isaki, Mulungu amene anandidyetsa ine nthawi zonse za moyo wanga kufikira lero, mthenga amene anandiombola ine ku zoipa zonse, adalitse anyamatawa; dzina langa litchulidwe pa iwo, ndi dzina la makolo anga Abrahamu ndi Isaki; iwo akule, nakhale khamu pakati pa dziko lapansi. Ndipo pamene Yosefe anaona kuti atate wake anaika dzanja lake lamanja pa mutu wa Efuremu, kudamuipira iye; ndipo anatukula dzanja la atate wake, kulichotsa pa mutu wa Efuremu ndi kuliika pa mutu wa Manase. Ndipo Yosefe anati kwa atate wake, Msatero atate wanga, chifukwa uyu ndi woyamba; ikani dzanja lanu lamanja pa mutu wake. Koma anakana atate wake, nati, Ndidziwa mwananga, ndidziwa; iyenso adzakhala mtundu wa anthu, iyenso adzakula; koma mphwake adzakhala wamkulu ndi iye, ndipo mbeu zake zidzakhala mitundu yambirimbiri. Ndipo anadalitsa iwo tsiku lomwelo, nati, Mwa iwe Israele adzadalitsa, kuti, Mulungu akuyese iwe monga Efuremu ndi monga Manase; ndipo anaika Efuremu woyamba wa Manase. Ndipo Israele anati kwa Yosefe, Taona, ndilinkufa ine; Mulungu adzakhala ndi iwe, adzakubwezanso iwe ku dziko la makolo ako. Ndipo ine ndakupatsa iwe gawo limodzi loposa la abale ako, limene ndinalanda m'dzanja la Aamori ndi lupanga langa ndi uta wanga. Ndipo Yakobo anaitana ana ake amuna, nati, Sonkhanani inu, kuti ndikuuzeni inu chimene chidzakugwerani inu masiku akudzawo. Sonkhanani, tamvani, ana amuna a Yakobo; tamverani Israele atate wanu. Rubeni, ndiwe woyamba wanga, mphamvu yanga ndi chiyambi cha mphamvu yanga; ulemu wopambana, ndi mphamvu yopambana. Wobwabwada ngati madzi; sudzapambana; chifukwa unakwera pa kama wa atate wako; pamenepo unaipitsapo; anakwera paja ndigonapo. Simeoni ndi Levi ndiwo abale; zida za mphulupulu ndizo malupanga ao. Mtima wangawe, usalowe mu chiungwe chao; ulemerero wanga, usadziphatike pa masonkhano ao; chifukwa m'kukwiya kwao anapha munthu. M'kufuna kwao anapundula ng'ombe. Kutembereredwe kukwiya kwao, chifukwa kunali koopsa; ndi kupsa mtima kwao, chifukwa kunali kwankhalwe. Ndidzawagawanitsa m'Yakobo. Ndidzabalalitsa iwo m'Israele. Yuda, abale ako adzakuyamika iwe; dzanja lako lidzakhala pa khosi la adani ako; ana amuna a atate wako adzakuweramira. Yuda ndi mwana wa mkango, kuchokera kuzomotola, mwananga, wakwera; anawerama pansi, anabwatama ngati mkango, ndipo ngati mkango waukazi; ndani adzamukitsa iye? Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye. Adamanga mwana wa kavalo wake pampesa, ndi mwana wa bulu wake pa mpesa wosankhika; natsuka malaya ake m'vinyo, ndi chofunda chake m'mwazi wa mphesa. Maso ake adzafiira ndi vinyo, ndipo mano ake adzayera ndi mkaka. Zebuloni adzakhala m'mphepete mwa nyanja; ndipo iye adzakhala dooko la ngalawa; ndipo malire ake adakhala pa Sidoni. Isakara ndiye bulu wolimba, alinkugona pakati pa makola. Ndipo anaona popumulapo kuti panali pabwino, ndi dziko kuti linali lokondweretsa; ndipo anaweramitsa phewa lake kuti anyamule, nakhala kapolo wakugwira ntchito ya msonkho. Dani adzaweruza anthu ake, monga limodzi la mafuko a Israele. Dani adzakhala njoka m'khwalala, songo panjira, imene iluma zitende za kavalo, kuti womkwera wake agwe chambuyo. Ndadikira chipulumutso chanu, Yehova. Ndi Gadi, achifwamba adzampsinja iye; koma iye adzapsinja pa chitende chao. Ndi Asere, chakudya chake ndicho mafuta, ndipo adzapereka zolongosoka zachifumu. Nafutali ndi mbawala yomasuka; apatsa mau abwino. Yosefe ndi nthambi yobala, nthambi yobala pambali pa kasupe; nthambi zake ziyangayanga palinga. Eni uta anavutitsa iye kwambiri, namponyera iye, namzunza. Koma uta wake unakhala wamphamvu, ndi mikono ya manja ake inalimbitsidwa. Ndi manja a Wamphamvu wa Yakobo. (Kuchokera kumeneko ndi mbusa, mwala wa Israele,) Ndi Mulungu wa atate wako amene adzakuthangata iwe, ndi Wamphamvuyonse, amene adzakudalitsa iwe. Ndi madalitso a Kumwamba, madalitso a madzi akuya akukhala pansi, madalitso a mawere, ndi a mimba. Madalitso a atate wako apambana mphamvu ndi madalitso a makolo anga, aufikira ku malekezero a patali a mapiri a chikhalire. Adzakhala pa mutu wa Yosefe, ndi pakati pa mutu wa iye amene ali wolekanitsidwa ndi abale ake. Benjamini ndiye mmbulu wakulusalusa; m'mamawa adzadya chomotola, madzulo adzagawa zofunkha. Awa onse ndiwo mafuko khumi ndi awiri a Israele: izo ndizo zomwe ananena kwa iwo atate wao nawadalitsa; yense monga mdalitso wake anawadalitsa. Ndipo analangiza iwo nati kwa iwo, Ine nditi ndisonkhanizidwe kwa anthu a mtundu wanga; mundiike ine pamodzi ndi makolo anga m'phanga lili m'munda wa Efuroni Muhiti, m'phanga lili m'munda wa Makipela, umene uli patsogolo pa Mamure, m'dziko la Kanani, limene Abrahamu analigula kwa Efuroni Muhiti pamodzi ndi munda, likhale poikira pake: pamenepo anaika Abrahamu ndi Sara mkazi wake; pamenepo anaika Isaki ndi Rebeka mkazi wake: pamenepo ndinaika Leya: munda ndi phanga lili m'menemo, zinagulidwa kwa ana a Hiti Pamene Yakobo anatha kulangiza ana ake amuna, anafunya mapazi ake pakama, natsirizika, nasonkhanizidwa kwa anthu a mtundu wake. Ndipo Yosefe anagwa pa nkhope ya atate wake, namlirira iye nampsompsona iye. Ndipo Yosefe anauza akapolo ake asing'anga kuti akonze atate wake ndi mankhwala osungira thupi: ndipo asing'anga anakonza Israele. Ndipo anatha masiku ake makumi anai a iye; chifukwa chomwecho amatsiriza masiku akukonza thupi; ndipo Aejipito anamlira iye masiku makumi asanu ndi awiri. Atapita masiku akumlira iye, Yosefe anati kwa mbumba ya Farao, kuti, Ngatitu ndapeza ufulu pamaso panu, nenanitu m'makutu a Farao kuti, Atate wanga anandilumbiritsa ine, kuti, Taona, ndilinkufa; m'manda m'mene ndadzikonzeratu ndekha m'dziko la Kanani, m'menemo udzandiika ine. Tsopano mundiloletu, ndikwereko, ndipite, ndikaike atate wanga, nditatero ndidzabweranso. Ndipo Farao anati, Pita, kaike atate wako, monga iye anakulumbiritsa iwe. Ndipo Yosefe anapita kukaika atate wake; ndipo anakwera pamodzi ndi akapolo onse a Farao, ndi akulu a pa mbumba yake, ndi akulu onse a m'dziko la Ejipito, ndi mbumba yonse ya Yosefe ndi abale ake, ndi mbumba ya atate wake: ang'ono ao okha, ndi nkhosa zao, ndi ng'ombe zao, anazisiya m'dziko la Goseni. Ndipo anakwera pamodzi ndi iye magaleta ndi apakavalo; ndipo panali khamu lalikulu. Ndipo anafika pa dwale la Atadi, lili tsidya lija la Yordani, pamenepo anamlira maliro a atate wake masiku asanu ndi limodzi. Ndipo pamene anthu okhala m'dzikomo, Akanani, anaona maliro a m'dwale la Atadi, anati, Awa ndi maliro akulu a Aejipito: chifukwa chake dzina la pamenepo linatchedwa Abele-Mizraimu, pali tsidya lija la Yordani. Ndipo ana ake amuna anamchitira iye monga anawalamulira iwo; chifukwa kuti ana ake amuna anamnyamula iye kulowa naye m'dziko la Kanani, ndi kumuika iye m'phanga la munda wa Makipela, limene Abrahamu analigula pamodzi ndi munda, likhale poikira pake, kwa Efuroni Muhiti, patsogolo pa Mamure. Ndipo ataika atate wake, Yosefe anabwera ku Ejipito, iye ndi abale ake, ndi onse amene anakwera pamodzi naye kukaika atate wake. Ndipo pamene abale ake a Yosefe anaona kuti atate wao anafa, anati, Kapena Yosefe adzatida ife, ndipo adzatibwezera ife zoipa zonse tidamchitira iye. Ndipo anatumiza mthenga kwa Yosefe kuti, Atate wathu asanafe analamulira, kuti, Muziti chotero kwa Yosefe, Mukhululukiretu tsopano kulakwa kwa abale anu, ndi kuchimwa kwao, chifukwa kuti anakuchitirani inu choipa; tsopano mutikhululukiretu kulakwa kwa akapolo a Mulungu wa atate wanu. Ndipo Yosefe analira pamene iwo ananena ndi iye. Ndiponso abale ake anamuka namgwadira pamaso pake; nati, Taonani, ife ndife akapolo anu. Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Musaope; pakuti ndili ine kodi m'malo a Mulungu? Koma inu, munandipangira ine choipa; koma Mulungu anachipangira chabwino, kuti kuchitike monga lero, kupulumutsa amoyo anthu ambiri. Ndipo tsopano musaope; ine ndidzachereza inu, ndi ana anu ang'ono. Ndipo anawatonthoza iwo mitima yao, nanena nao mokoma mtima. Ndipo Yosefe anakhala m'Ejipito, iye, ndi mbumba ya atate wake; ndipo Yosefe anakhala ndi moyo zaka zana limodzi ndi khumi. Ndipo Yosefe anaona ana a Efuremu a mbadwo wachitatu; ananso a Makiri mwana wamwamuna wa Manase anabadwa pa maondo a Yosefe. Yosefe ndipo anati kwa abale ake, Ndilinkufa ine, koma Mulungu adzaonekera kwa inu, adzakuchotsani inu m'dziko muno kubwera kunka ku dziko limene analumbirira kwa Abrahamu ndi kwa Isaki, ndi kwa Yakobo. Ndipo Yosefe analumbiritsa ana a Israele kuti, Mulungu adzaonekera kwa inu ndithu, ndipo mudzakwera nao mafupa anga kuchokera kuno. Ndipo anafa Yosefe, anali wa zaka zana limodzi ndi khumi; ndipo anakonza thupi lake ndi mankhwala osungira, ndipo anamuika iye m'bokosi m'Ejipito. Ndipo maina a ana a Israele, amene analowa m'Ejipito ndi Yakobo ndi awa, analowa munthu ndi banja lake: Rubeni, Simeoni, Levi ndi Yuda; Isakara, Zebuloni, ndi Benjamini; Dani ndi Nafutali, Gadi ndi Asere. Ndipo amoyo onse amene anatuluka m'chuuno mwake mwa Yakobo ndiwo makumi asanu ndi awiri; koma Yosefe anali m'Ejipito. Ndipo anafa Yosefe, ndi abale ake onse, ndi mbadwo uwo wonse. Ana a Israele ndipo anaswana, nabalana, nachuluka, nakhala nazo mphamvu zazikulu; ndipo dziko linadzala nao. Pamenepo inalowa mfumu yatsopano m'ufumu wa Ejipito, imene siinadziwa Yosefe. Ndipo ananena ndi anthu ake, Taonani, anthu, ndiwo ana a Israele, achuluka, natiposa mphamvu. Tiyeni, tiwachenjerere angachuluke, ndi kuphatikizana ndi adani athu ikafika nkhondo, ndi kulimbana nafe, ndi kuchoka m'dzikomo. Potero anawaikira akulu a misonkho kuti awasautse ndi akatundu ao. Ndipo anammangira Farao midzi yosungiramo chuma, ndiyo Pitomu ndi Ramsesi. Koma monga momwe anawasautsiramo, momwemo anachuluka, momwemonso anafalikira. Ndipo anavutika chifukwa cha ana Israele. Ndipo Aejipito anawagwiritsa ana a Israele ntchito yosautsa; nawawitsa moyo wao ndi ntchito yolimba, ya dothi ndi ya njerwa, ndi ntchito zonse za pabwalo, ntchito zao zonse zimene anawagwiritsa nzosautsa. Ndipo mfumu ya Aejipito inanena ndi anamwino a Ahebri, dzina lake la wina ndiye Sifira, dzina la mnzake ndiye Puwa; ninati, Pamene muchiza akazi a Ahebri nimuwaone pamipando; akakhala mwana wamwamuna, mumuphe; akakhala wamkazi, akhale ndi moyo. Koma anamwino anaopa Mulungu, ndipo sanachite monga mfumu ya Aejipito inawauza, koma analeka ana amuna akhale ndi moyo. Ndipo mfumu ya Aejipito inaitana anamwino, ninena nao, Mwachita ichi chifukwa ninji, ndi kuleka ana amunawo akhale ndi moyo? Ndipo anamwino ananena ndi Farao, Popeza akazi a Ahebri safanana ndi akazi a Aejipito; pakuti ali ndi mphamvu, naona ana asanafike anamwino. Potero Mulungu anawachitira zabwino anamwino; ndipo anthuwo anachuluka, nakhala nazo mphamvu zazikulu. Ndipo kunatero kuti, popeza anamwino anaopa Mulungu, Iye anawamangitsira mabanja. Ndipo Farao analamulira anthu ake onse, ndi kuti, Ana amuna onse akabadwa aponyeni m'nyanja, koma ana akazi onse alekeni amoyo. Ndipo anamuka munthu wa banja la Levi, natenga mwana wamkazi wa Levi. Ndipo anaima mkaziyo, naona mwana wamwamuna; m'mene anamuona kuti ali wokoma, anambisa miyezi itatu. Koma pamene sanathe kumbisanso, anamtengera kabokosi kagumbwa, napakapo nkhunga ndi phula; naikamo mwanayo, nakaika pakati pa mabango m'mbali mwa nyanja. Ndipo mlongo wake anaima patali, adziwe chomwe adzamchitira. Ndipo mwana wamkazi wa Farao anatsikira kukasamba m'nyanja; ndipo atsikana ake anayendayenda m'mbali mwa nyanja; ndipo iye anaona kabokosi pakati pa mabango, natuma mdzakazi wake akatenge. Pamene anakavundukula, anapenya mwanayo; ndipo taonani, khandalo lilikulira. Ndipo anamva naye chifundo, nati, Uyu ndiye wa ana a Ahebri. Pamenepo mlongo wake ananena ndi mwana wamkazi wa Farao, Ndipite ine kodi kukuitanirani woyamwitsa wa Ahebri, akuyamwitsireni mwanayo? Ndipo mwana wamkazi wa Farao ananena naye, Pita. Napita namwaliyo, nakaitana amake wa mwanayo. Ndipo mwana wamkazi wa Farao ananena naye, Pita naye mwana uyu, ndi kundiyamwitsira iye, ndidzakupatsa mphotho yako. Ndipo mkaziyo anatenga mwanayo, namyamwitsa. Ndipo atakula mwanayo, anapita naye kwa mwana wamkazi wa Farao, ndipo iye anakhala mwana wake. Ndipo anamutcha dzina lake Mose, nati, Chifukwa ndinamvuula m'madzi. Ndipo kunali masiku amenewo, atakula Mose, kuti anatulukira kukazonda abale ake, napenya akatundu ao; ndipo anaona munthu Mwejipito ali kukantha Muhebri, wa abale ake. Ndipo anaunguza kwina ndi kwina, ndipo pamene anaona kuti palibe munthu, anakantha Mwejipito, namfotsera mumchenga. M'mawa mwake anatulukanso, ndipo, taonani, anthu awiri Ahebri alikugwirana; ndipo ananena ndi wochimwayo, kuti, Umpandiranji mnzako? Koma anati, Wakuika iwe ndani ukhale mkulu ndi woweruza wathu? Kuteroku ukuti undiphe, monga unamupha Mwejipito? Ndipo Mose anachita mantha, nanena, Ndithu chinthuchi chadziwika. Pamene Farao anachimva ichi, anafuna kupha Mose. Koma Mose anathawa pankhope pa Farao, nakhala m'dziko la Midiyani; nakhala pansi pachitsime. Ndipo wansembe wa Midiyani anali nao ana akazi asanu ndi awiri, amene anadza kudzatunga madzi; ndipo anadzaza mimwero kuti amwetse gulu la atate wao. Pamenepo anadza abusa nawapirikitsa; koma Mose anauka nawathandiza, namwetsa gulu lao. M'mene anafika kwa Reuwele atate wao, iye anati, Mwabwera msanga bwanji lero? Ndipo anati iwo, Munthu Mwejipito anatilanditsa m'manja a abusa, natitungiranso madzi okwanira, namwetsa gululi. Ndipo anati kwa ana ake akazi, Ali kuti iye? Mwamsiyiranji munthuyo? Kamuitaneni, adzadye chakudya. Ndipo Mose anavomera kukhala naye munthuyo; ndipo anampatsa Mose mwana wake wamkazi Zipora. Ndipo anaona mwana, ndi Mose anamutcha dzina lake Geresomo; pakuti anati, Ndakhala mlendo m'dziko la eni. Ndipo kunali pakupita masiku ambiri aja, idafa mfumu ya Aejipito; ndi ana a Israele anatsitsa moyo chifukwa cha ukapolo wao, nalira, ndi kulira kwao kunakwera kwa Mulungu chifukwa cha ukapolowo. Ndipo Mulungu anamva kubuula kwao, ndi Mulungu anakumbukira chipangano chake ndi Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo. Ndipo Mulungu anapenya Aisraele, ndi Mulungu anadziwa. Koma Mose analikuweta gulu la Yetero mpongozi wake, wansembe wa ku Midiyani; natsogolera gululo m'tsogolo mwa chipululu, nafika kuphiri la Mulungu, ku Horebu. Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera m'chilangali chamoto chotuluka m'kati mwa chitsamba; ndipo anapenya, ndipo taonani, chitsamba chilikuyaka moto, koma chosanyeka chitsambacho. Ndipo Mose anati, Ndipatuketu, ndikaone chooneka chachikulucho, chitsambacho sichinyeka bwanji. Pamene Yehova anaona kuti adapatuka kukapenya, Mulungu ali m'kati mwa chitsamba, anamuitana, nati, Mose, Mose. Ndipo anati, Ndili pano. Ndipo Iye anati, Usayandikire kuno; vula nsapato zako ku mapazi ako, pakuti pamalo pamene upondapo iwe, mpopatulika. Ananenanso, Ine ndine Mulungu wa atate wako, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo. Ndipo Mose anabisa nkhope yake; popeza anaopa kuyang'ana Mulungu. Ndipo Yehova anati, Ndapenyetsetsa mazunzo a anthu anga ali m'Ejipito, ndamvanso kulira kwao chifukwa cha akuwafulumiza; pakuti ndidziwa zowawitsa zao; ndipo ndatsikira kuwalanditsa m'manja a anthu a Ejipito, ndi kuwatulutsa m'dziko lija akwere nalowe m'dziko labwino ndi lalikulu, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ku malo a Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi. Ndipo tsopano, taona kulira kwa ana a Israele kwandifikira; ndapenyanso kupsinjika kumene Aejipito awapsinja nako. Tiye tsopano, ndikutuma kwa Farao, kuti utulutse anthu anga, ana a Israele m'Ejipito. Koma Mose anati kwa Mulungu Ndine yani ine kuti ndipite kwa Farao, ndi kuti nditulutse ana a Israele m'Ejipito? Ndipo Iye anati, Ine ndidzakhala ndi iwe; ndipo ichi ndi chizindikiro cha iwe, chakuti ndakutuma ndine; utatulutsa anthuwo m'Ejipito, mudzatumikira Mulungu paphiri pano. Ndipo Mose anati kwa Mulungu, Onani, pakufika ine kwa ana a Israele, ndi kunena nao, Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu; ndipo akakanena ndi ine, Dzina lake ndani? Ndikanena nao chiyani? Ndipo Mulungu anati kwa Mose, INE NDINE YEMWE NDILI INE. Anatinso, Ukatero ndi ana a Israele, INE NDINE wandituma kwa inu. Ndipo Mulungu ananenanso kwa Mose, Ukatero ndi ana a Israele, Yehova Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo anandituma kwa inu; ili ndi dzina langa nthawi yosatha, ichi ndi chikumbukiro changa m'mibadwomibadwo. Muka, nukasonkhanitse akulu a Israele, nunene nao, Yehova, Mulungu wa makolo anu anandionekera ine, Mulungu wa Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, ndi kuti, Ndakuzondani ndithu, ndi kuona chomwe akuchitirani m'Ejipito; ndipo ndanena, Ndidzakukwezani kukutulutsani m'mazunzo a Aejipito, kukulowezani m'dziko la Akanani, ndi Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi. Ndipo adzamvera mau ako; ndipo ukapite iwe ndi akulu a Israele, kwa mfumu ya Aejipito, ndi kukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri wakomana ndi ife; tiloleni, timuke tsopano ulendo wa masiku atatu m'chipululu, kuti timphere nsembe Yehova Mulungu wathu. Koma Ine ndidziwa kuti mfumu ya Aejipito siidzalola inu kumuka, inde lingakhale ndi dzanja lamphamvu ai. Ndipo ndidzatambasula dzanja langa, ndi kukantha Aejipito ndi zozizwa zanga zonse ndizichita pakati pake; ndi pambuyo pake adzakulolani kumuka. Ndipo ndidzapatsa anthu awa ufulu pamaso pa anthu a Ejipito; ndipo kudzakhala, pamene mutuluka simudzatuluka opanda kanthu; koma mkazi yense adzafunse mnzake, ndi mlendo wokhala m'nyumba mwake, ampatse zokometsera zasiliva, ndi zokometsera zagolide, ndi zovala; ndipo mudzaveke nazo ana anu aamuna ndi aakazi; ndipo mudzafunkhe za Aejipito. Ndipo Mose anayankha nati, Koma taonani, sadzakhulupirira ine, kapena kumvera mau anga; pakuti adzanena, Yehova sanakuonekere iwe. Ndipo Yehova ananena naye, Icho nchiyani m'dzanja lako? Nati, Ndodo. Ndipo ananena Iye, Iponye pansi. Naiponya pansi, ndipo inasanduka njoka; ndipo Mose anaithawa. Koma Yehova anati kwa Mose, Tambasula dzanja lako, nuigwire kumchira; ndipo anatambasula dzanja lake, naigwira, nikhalanso ndodo m'dzanja lake; kuti akhulupirire kuti wakuonekera Yehova Mulungu wa makolo ao, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo. Ndipo Yehova ananenanso naye, Longa dzanja lako pachifuwa pako. Ndipo analonga dzanja lake pachifuwa pake, nalitulutsa, taonani, dzanja lake linali lakhate, lotuwa ngati chipale chofewa. Ndipo ananena iye, Bwerezanso dzanja lako pachifuwa pako. Ndipo anabwerezanso dzanja lake pachifuwa pake; nalitulutsa pachifuwa pake, taonani, linasandukanso lomwe lakale. Ndipo kudzatero, ngati sakhulupirira iwe, ndi kusamvera mau a chizindikiro choyamba, adzakhulupirira mau a chizindikiro chotsirizachi. Ndipo kudzatero, akapanda kukhulupirira zingakhale zizindikiro izi, ndi kusamvera mau ako, ukatunge madzi a kunyanja ndi kuthira pamtunda; ndi madzi watunga ku nyanjayo adzasanduka mwazi pamtunda. Ndipo Mose anati kwa Yehova, Mverani, Ambuye, ine ndine munthu wosowa ponena, kapena dzulo, kapena kale, kapena chilankhulire Inu ndi kapolo wanu, pakuti ndine wa m'kamwa molemera, ndi wa lilime lolemera. Koma Yehova ananena naye, Anampangira munthu m'kamwa ndani? Kapena analenga munthu wosalankhula ndani, kapena wogontha, kapena wamaso, kapena wakhungu? Si ndine Yehova kodi? Ndipo tsopano muka, ndipo Ine ndidzakhala m'kamwa mwako, ndi kukuphunzitsa chomwe ukalankhule. Koma anati, Mverani, Ambuye, tumizani pa dzanja la iye amene mudzamtuma. Pamenepo mkwiyo wa Yehova unamyakira Mose, ndipo anati, Nanga Aroni Mlevi mbale wako sialipo kodi? Ndidziwa kuti kulankhula alankhula. Ndipo, taona, atuluka kudzakomana ndiwe; ndipo pakuona iwe adzakondwera m'mtima mwake. Ndipo ukalankhule naye, ndi kumpangira mau; ndipo Ine ndidzakhala m'kamwa mwako, ndi m'kamwa mwake, ndipo ndidzakuphunzitsani inu chimene mukachite. Ndipo iye adzakulankhulira iwe kwa anthu; ndipo kudzatero, kuti iye adzakhala kwa iwe ngati m'kamwa, ndi iwe udzakhala kwa iye ngati Mulungu. Ndipo ukaigwire m'dzanja lako ndodo iyi, imene ukachite nayo zizindikirozo. Ndipo Mose anabwera namuka kwa Yetero mpongozi wake, nanena naye, Ndimuketu, ndibwerere kunka kwa abale anga amene ali m'Ejipito, ndikaone ngati akali ndi moyo. Ndipo Yetero ananena ndi Mose, Pita bwino. Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'Midiyani, Muka, bwerera kunka ku Ejipito; pakuti adafa anthu onse amene anafuna moyo wako. Pamenepo Mose anatenga mkazi wake ndi ana ake amuna, nawakweza pa bulu, nabwerera kunka ku dziko la Ejipito; ndipo Mose anagwira ndodo ya Mulungu m'dzanja lake. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Pakumuka iwe kubwerera kunka ku Ejipito, usamalire uchite zozizwa zonse ndaziika m'dzanja lako, pamaso pa Farao; koma Ine ndidzalimbitsa mtima wake kuti asadzalole anthu kupita. Pamenepo ukanene ndi Farao, Atero Yehova Mwana wanga, mwana wanga woyamba ndiye Israele. Ndipo ndanena ndi iwe, Mlole mwana wanga amuke, kuti anditumikire Ine; koma wakana kumlola kuti asamuke; taona, Ine ndidzamupha mwana wako wamwamuna, mwana wako woyamba. Ndipo kunali panjira, kuchigono, Yehova anakomana naye, nafuna kumupha. Koma Zipora anatenga mpeni wamwala, nadula khungu la mwana wake, naliponya pa mapazi ake; nati, Pakuti iwe ndiwe mkwati wanga wamwazi. Ndipo Iye anamleka. Pamenepo anati mkaziyo, Mkwati wamwazi iwe, chifukwa cha mdulidwe. Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Muka kuchipululu kukakomana ndi Mose. Ndipo anamuka, nakomana naye pa phiri la Mulungu, nampsompsona. Ndipo Mose anauza Aroni mau onse a Yehova amene adamtuma nao, ndi zizindikiro zonse zimene adamlamulira. Pamenepo Mose ndi Aroni anamuka nasonkhanitsa akulu onse a ana a Israele; ndipo Aroni anawafotokozera mau onse amene Yehova adauza Mose, nachita zizindikiro zija pamaso pa anthu. Ndipo anthuwo anakhulupirira; ndipo pamene anamva kuti Yehova adawazonda ana a Israele, ndi kuti adaona mazunzo ao, anawerama, nalambira Mulungu. Ndipo pambuyo pake Mose ndi Aroni analowa nanena ndi Farao, Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Lola anthu anga apite, kundichitira madyerero m'chipululu. Koma Farao anati, Yehova ndani, kuti ndimvere mau ake ndi kulola Israele apite? Sindimdziwa Yehova, ndiponso sindidzalola Israele apite. Ndipo iwo anati, Mulungu wa Ahebri wakomana ndi ife; timuketu ulendo wa masiku atatu m'chipululu, kumphera nsembe Yehova Mulungu wathu; kuti angatikanthe ndi mliri, kapena ndi lupanga. Ndipo mfumu ya Aejipito inanena nao, Inu, Mose ndi Aroni, chifukwa ninji mumasulira anthu ntchito zao? Mukani ku akatundu anu. Farao anatinso, Taonani, anthu a m'dziko ndiwo ambiri tsopano; ndipo inu muwapumitsa ku akatundu ao. Ndipo tsiku lomwelo Farao analamulira akufulumiza anthu, ndi akapitao ao, ndi kuti, Musawapatsanso anthu udzu wakupanga nao njerwa monga kale; apite okha adzifunire udzu. Ndipo muziwawerengera njerwa, monga momwe anapanga kale; musachepsapo, popeza achita chilezi; chifukwa chake alikufuula, ndi kuti, Timuke, timphere nsembe Mulungu wathu. Ilimbike ntchito pa amunawo, kuti aigwiritsitse, asasamalire mau amabodza. Ndipo akufulumiza anthu ndi akapitao ao anatuluka, nanena ndi anthu ndi kuti, Atero Farao, Kulibe kukupatsani udzu. Mukani inu nokha, dzifunireni udzu komwe muupeza; pakuti palibe kanthu kadzachepa pa ntchito yanu. Pamenepo anthuwo anabalalika m'dziko lonse la Ejipito kufuna chiputu ngati udzu. Ndipo akufulumiza anawakakamiza, ndi kuti, Tsirizani ntchito zanu, ntchito ya tsiku pa tsiku lake, monga muja munali ndi udzu. Ndipo anapanda akapitao a ana a Israele, amene ofulumiza a Farao adawaika, ndi kuti, Nanga dzulo ndi lero simunatsiriza bwanji ntchito yanu yoneneka ya njerwa, monga kale? Pamenepo akapitao a ana a Israele anafika nalirira Farao, nati, Mwatero bwanji ndi akapolo anu? Udzu osawapatsa akapolo anu, ndipo amanena ndi ife, Umbani njerwa; ndipo, taonani, amapanda akapolo anu; koma kulakwa nkwa anthu anu. Koma iye anati, Aulesi inu, aulesi: chifukwa chake mulikunena, Timuke, timphere nsembe Yehova. Mukani tsopano, gwirani ntchito; pakuti sadzakupatsani udzu, koma muonetse chiwerengero chake cha njerwa. Ndipo akapitao a ana a Israele anaona kuti kudawaipira, pamene ananena, Musamachepetsa njerwa zanu, ntchito ya tsiku pa tsiku lake. Ndipo potuluka kwa Farao iwo anakomana ndi Mose ndi Aroni, alikuima popenyana nao; ndipo ananena nao, Yehova akupenyeni, naweruze; pakuti mwatinyansitsa pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake, ndi kuwapatsa lupanga m'dzanja lao kutipha nalo. Pamenepo Mose anabwerera namka kwa Yehova, nati, Ambuye, mwawachitiranji choipa anthuwa? Mwandituma bwanji? Popeza kuyambira kuja ndinafika kwa Farao kulankhula m'dzina lanu, anawachitira choipa anthuwa; ndipo simunalanditsa anthu anu konse. Ndipo Yehova ananena kwa Mose, Tsopano udzaona chomwe ndidzachitira Farao; pakuti ndi dzanja lamphamvu adzawalola apite, inde ndi dzanja lamphamvu adzawaingitsa m'dziko lake. Ndipo Mulungu ananena ndi Mose, nati kwa iye, Ine ndine YEHOVA: ndipo ndinaonekera Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, Mulungu Wamphamvuyonse; koma sindinadziwika kwa iwo ndi dzina langa YEHOVA. Ndipo ndinakhazikitsanso nao chipangano changa, kuwapatsa dziko la Kanani, dziko la maulendo ao, anali alendo m'mwemo. Ndamvanso kubuula kwa ana a Israele, amene Aejipito awayesa akapolo; ndipo ndakumbukira chipangano changa. Chifukwa chake nena kwa ana a Israele Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakutulutsani pansi pa akatundu a Aejipito ndipo ndidzakulanditsani ku ukapolo wanu; ndipo ndidzakuombolani ndi dzanja lotambasuka, ndi maweruzo akulu; ndipo ndidzalandira inu mukhale anthu anga, ndipo ndidzakhala Ine Mulungu wanu; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, wakutulutsa inu pansi pa akatundu a Aejipito. Ndipo ndidzakulowetsani m'dziko limene ndinakweza dzanja langa kunena za ilo, kuti ndilipereke kwa Abrahamu, kwa Isaki ndi kwa Yakobo; ndipo ndidzakupatsani ilo likhale lanulanu; Ine ndine Yehova. Ndipo Mose ananena chomwecho ndi ana a Israele; koma sanamvere Mose chifukwa cha kuwawa mtima, ndi ukapolo wolemera. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Lowa, lankhula ndi Farao mfumu ya Aejipito, kuti alole ana a Israele atuluke m'dziko lake. Koma Mose ananena pamaso pa Yehova, ndi kuti, Onani, ana a Israele sanandimvere ine; adzandimvera bwanji Farao, ndine wa milomo yosadula? Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nawalangiza za ana a Israele, ndi za Farao mfumu ya Aejipito, kuti atulutse ana a Israele m'dziko la Ejipito. Akulu a mbumba za makolo ao ndi awa: ana amuna a Rubeni, woyamba wa Israele ndiwo: Hanoki ndi Palu, Hezironi, ndi Karimi; amene ndiwo mabanja a Rubeni. Ndi ana amuna a Simeoni ndiwo: Yemuwele, ndi Yamini, ndi Ohadi, Yakini, ndi Zohari, ndi Shaulo mwana wa mkazi wa Mkanani; amene ndiwo mabanja a Simeoni. Ndipo maina a ana amuna a Levi, mwa kubadwa kwao ndiwo: Geresoni, ndi Kohati, ndi Merari; ndipo zaka za moyo wa Levi ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri. Ana amuna a Geresoni ndiwo: Libini ndi Simei, mwa mabanja ao. Ndi ana amuna a Kohati ndiwo: Amuramu ndi Izihara, ndi Hebroni, ndi Uziyele; ndipo zaka za moyo wa Kohati ndizo zana limodzi ndi makumi atatu ndi kudza zitatu. Ndipo ana amuna a Merari ndiwo: Mali ndi Musi. Amenewo ndiwo mabanja a Levi mwa kubadwa kwao. Ndipo Amuramu anadzitengera Yokebede mlongo wa atate wake akhale mkazi wake; ndipo anambalira Aroni ndi Mose; ndi zaka za moyo wa Amuramu ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri. Ndi ana amuna a Izihara ndiwo: Kora ndi Nefegi, ndi Zikiri. Ndi ana amuna a Uziyele ndiwo: Misaele, ndi Elizafani, ndi Sitiri. Ndipo Aroni anadzitengera Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wake wa Nasoni, akhale mkazi wake; ndipo anambalira Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara. Ndipo ana amuna a Kora ndiwo: Asiri ndi Elikana, ndi Abiyasafu; amenewo ndiwo mabanja a Akora. Ndipo Eleazara mwana wa Aroni anadzitengera mkazi wa ana akazi a Putiyele akhale mkazi wake, ndipo anambalira Finehasi. Amenewo ndi akulu a makolo a Alevi mwa mabanja ao. Omwewo ndiwo Aroni ndi Mose amene Yehova ananena nao, Tulutsani ana a Israele m'dziko la Ejipito mwa makamu ao. Awa ndi omwewo ananena ndi Farao, mfumu ya Aejipito, awatulutse ana a Israele m'Ejipito; Mose ndi Aroni amenewa. Ndipo kunali, tsiku limene Yehova ananena ndi Mose m'dziko la Ejipito, Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Ine ndine Yehova; lankhula ndi Farao mfumu ya Aejipito zonsezi Ine ndizinena nawe. Koma Mose anati pamaso pa Yehova, Onani, ine ndili wa milomo yosadula ndipo Farao adzandimvera bwanji? Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Taona, ndakuika ngati Mulungu kwa Farao; ndi Aroni mkulu wako adzakhala mneneri wako. Iwe uzilankhula zonse ndikulamulira; ndi Aroni mkulu wako azilankhula kwa Farao, kuti alole ana a Israele atuluke m'dziko lake. Koma Ine ndidzaumitsa mtima wake wa Farao, ndipo ndidzachulukitsa zizindikiro ndi zozizwa zanga m'dziko la Ejipito. Koma Farao sadzamvera inu, ndipo ndidzaika dzanja langa pa Aejipito, ndipo ndidzatulutsa makamu anga, anthu anga ana a Israele, m'dziko la Ejipito ndi maweruzo akulu. Ndipo Aejipito adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakutambasula Ine dzanja langa pa Aejipito, ndikutulutsa ana a Israele pakati pao. Ndipo Mose ndi Aroni anachita monga Yehova anawalamulira, momwemo anachita. Ndipo Mose anali nazo zaka makumi asanu ndi atatu, ndi Aroni anali nazo zaka makumi asanu ndi atatu kudza zitatu, pamene ananena ndi Farao. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, ndi kuti, Pamene Farao adzalankhula nanu, ndi kuti, Dzichitireni chodabwitsa; pamenepo uzinena ndi Aroni, Tenga ndodo yako, iponye pansi pamaso pa Farao, isanduke chinjoka. Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao, nachita monga momwe Yehova adawalamulira; ndipo Aroni anaponya pansi ndodo yake pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake, ndipo inasanduka chinjoka. Pamenepo Farao anaitananso anzeru, ndi amatsenga; ndipo alembi a Aejipito, iwonso anachita momwemo ndi matsenga ao. Pakuti yense anaponya pansi ndodo yake, ndipo zinasanduka zinjoka; koma ndodo ya Aroni inameza ndodo zao. Koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvere iwo; monga adalankhula Yehova. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Walemera mtima wa Farao, akana kulola anthu apite. Muka kwa Farao m'mawa; taona, atuluka kunka kumadzi; nuime kumlinda m'mbali mwa nyanja; ndi ndodo idasanduka njokayo uigwire m'dzanja lako. Ndipo ukanena naye, Yehova, Mulungu wa Ahebri anandituma kwa inu, ndi kuti, Lola anthu anga amuke kuti anditumikire m'chipululu; koma, taona, sunamvera ndi pano. Atero Yehova, Ndi ichi udzadziwa kuti Ine ndine Yehova; taonani, ndidzapanda madzi ali m'nyanja ndi ndodo ili m'dzanja langa, ndipo adzasanduka mwazi. Ndi nsomba zili m'nyanja zidzafa, ndi nyanja idzanunkha; ndi Aejipito adzachita mtima useru ndi kumwa madzi a m'nyanjamo. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Tenga ndodo yako, nutambasule dzanja lako pa madzi a m'Ejipito, pa nyanja yao, pa ngalande zao, ndi pa matamanda ao, ndi pa matawale ao onse amadzi, kuti asanduke mwazi; mukhale mwazi m'dziko lonse la Ejipito, m'zotengera zamtengo, ndi zamwala. Ndipo Mose ndi Aroni anachita monga momwe Yehova adawalamulira; nasamula ndodo, napanda madzi ali m'nyanjamo pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake; ndipo madzi onse a m'nyanjamo anasanduka mwazi. Ndi nsomba za m'nyanjamo zinafa; ndi nyanjayo inanunkha; ndipo Aejipito sanakhoze kumwa madzi a m'nyanjamo; ndipo munali mwazi m'dziko lonse la Ejipito. Ndipo alembi a Aejipito anachita momwemo ndi matsenga ao; koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvere iwo; monga adalankhula Yehova. Ndipo Farao anatembenuka, nalowa m'nyumba yake, osasamalira ichi chomwe mumtima mwake. Koma Aejipito onse anakumba m'mphepete mwa nyanja kufuna madzi akumwa; pakuti sanakhoze kumwa madzi a m'nyanjamo. Ndipo anafikira masiku asanu ndi awiri atapanda nyanja Yehova. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwa Farao, nunene naye, Atero Yehova, Lola anthu anga amuke, kuti anditumikire. Ndipo ukakana kuwalola amuke, taona, Ine ndidzapanda dziko lako lonse ndi achule; ndipo m'nyanjamo mudzachuluka achule, amene adzakwera nadzalowa m'nyumba mwako, ndi m'chipinda chogona iwe, ndi pakama pako, ndi m'nyumba ya anyamata ako, ndi pa anthu ako, m'michembo yanu yoocheramo, ndi m'mbale zanu zoumbiramo. Ndipo achule adzakwera pa iwe, ndi pa anthu ako, ndi pa anyamata ako onse. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Tambasula dzanja lako ndi ndodo yako, panyanja, pangalande, ndi pamatamanda, nukweretse achule pa dziko la Ejipito. Ndipo Aroni anatambasula dzanja lake pa madzi a m'Ejipito; ndipo anakwera achule, nakuta dziko la Ejipito. Ndipo alembi anachita momwemo ndi matsenga ao, nakweretsa achule pa dziko la Ejipito. Pamenepo Farao anaitana Mose ndi Aroni, nati, Mundipembere Yehova, kuti andichotsere ine ndi anthu anga achulewo; ndipo ndidzalola anthu amuke, kuti amphere Yehova nsembe. Koma Mose anati kwa Farao, Ulemu ndi wanu, wa ine ai; ndipembere inu ndi anyamata anu ndi anthu anu liti, kuti aonongeke achulewo, achokere inu ndi nyumba zanu, atsale m'nyanja mokha? Ndipo anati, Mawa. Nati Mose, Kukhale monga mau anu, kuti muziwe, kuti palibe wina wonga Yehova Mulungu wathu. Ndipo achule adzachokera inu, ndi nyumba zanu, ndi anyamata anu, ndi anthu anu; adzatsala m'nyanja mokha. Ndipo Mose ndi Aroni anatuluka kwa Farao; ndi Mose anafuulira kwa Yehova kunena za achule amene adawaika pa Farao. Ndipo Yehova anachita monga mwa mau a Mose; nafa achulewo kuchokera m'zinyumba, ndi m'mabwalo, ndi m'minda. Ndipo anawaola miulumiulu; ndi dziko linanunkha. Koma pamene Farao anaona kuti panali kupuma, anaumitsa mtima wake, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Samula ndodo yako, nupande fumbi lapansi, kuti lisanduke nsabwe m'dziko lonse la Ejipito. Ndipo anachita chomwecho; pakuti Aroni anasamula dzanja lake ndi ndodo yake, napanda fumbi lapansi, ndipo panali nsabwe pa anthu ndi pa zoweta; fumbi lonse lapansi linasanduka nsabwe m'dziko lonse la Ejipito. Alembi anateronso ndi matsenga ao kuonetsa nsabwe, koma sanakhoza; ndipo panali nsabwe pa anthu, ndi pa zoweta. Pamenepo alembi anati kwa Farao, Chala cha Mulungu ichi; koma mtima wa Farao unalimba, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova. Ndipo Yehova anati kwa Mose Uuke ulawire mamawa, nuime pamaso pa Farao; taona, atuluka kunka kumadzi; nunene naye, Atero Yehova, Lola anthu anga amuke, anditumikire. Pakuti ukapanda kulola anthu anga amuke, taona, ndidzatuma mizaza pa iwe, ndi pa anyamata ako, ndi pa anthu ako, ndi pa nyumba zako; ndipo nyumba za Aejipito zidzadzala nayo mizaza, ndi nthaka yomwe imene ikhalapo. Ndipo tsiku ilo ndidzalemba malire dziko la Goseni, m'mene mukhala anthu anga, kuti pamenepo pasakhale mizaza; kotero kuti udziwe kuti Ine ndine Yehova pakati pa dzikoli. Ndipo ndidzaika chosiyanitsa pakati pa anthu anga ndi anthu ako; mawa padzakhala chizindikiro ichi. Ndipo Yehova anachita chomwecho; ndipo kunafika magulu a mizaza m'nyumba ya Farao, ndi m'nyumba za anyamata ake, ndi m'dziko lonse la Ejipito; dziko linaipatu chifukwa cha mizazayo. Pamenepo Farao anaitana Mose ndi Aroni, nati, Mukani, mphereni nsembe Mulungu wanu m'dzikomu. Koma Mose anati, Sikuyenera kutero; pakuti tidzamphera Yehova Mulungu wathu chonyansa cha Aejipito; taonani, ngati tikamphera nsembe chonyansa cha Aejipito pamaso pao sadzatiponya miyala kodi? Timuke ulendo wa masiku atatu m'chipululu, tikamphere Yehova Mulungu wathu nsembe, monga adzanena nafe. Ndipo Farao anati, Ndidzakulolani mumuke, kuti mukamphere nsembe Yehova Mulungu wanu m'chipululu; komatu musamuke kutalitu: mundipembere. Ndipo Mose anati, Onani, ndilikutuluka ine kwanu, ndidzapemba Yehova kuti mizaza ichoke mawa kwa Farao, ndi kwa anyamata ake, ndi kwa anthu ake; komatu, Farao asanyengenso ndi kukana kulola anthuwa amuke kukamphera nsembe Yehova. Ndipo Mose anatuluka kwa Farao, napemba Yehova. Ndipo Yehova anachita monga mwa mau a Mose; nachotsera Farao ndi anyamata ake ndi anthu ake mizazayo, sunatsala ndi umodzi wonse. Koma Farao anaumitsa mtima wake nthawi yomweyonso, ndipo sanalola anthu amuke. Pamenepo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwa Farao, numuuze, Atero Yehova Mulungu wa Ahebri, Lola anthu anga amuke, kuti anditumikire. Pakuti ukakana kuwalola amuke, ndi kuwagwira chigwiritsire, taona, dzanja la Yehova lidzakhala pa zoweta zako za kubusa, pa akavalo, pa abulu, pa ngamira, pa ng'ombe, ndi pa zoweta zazing'ono ndi kalira woopsa. Ndipo Yehova adzasiyanitsa pakati pa zoweta za Israele ndi zoweta za Ejipito; kuti kasafe kanthu kalikonse ka ana a Israele. Ndipo Yehova anaika nthawi yakuti, nati, Mawa Yehova adzachita chinthu ichi m'dzikomu. Ndipo m'mawa mwake Yehova anachita chinthucho, ndipo zinafa zoweta zonse za m'Ejipito; koma sichinafa chimodzi chonse cha zoweta za ana a Israele. Ndipo Farao anatuma, taonani, sichidafa chingakhale chimodzi chomwe cha zoweta za Aisraele. Koma mtima wa Farao unauma, ndipo sanalole anthu amuke. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, Tengani phulusa la ng'anjo lodzala manja; ndi Mose aliwaze kuthambo pamaso pa Farao. Ndipo lidzakhala fumbi losalala pa dziko lonse la Ejipito, ndipo lidzakhala pa anthu ndi pa zoweta ngati zilonda zobuka ndi matuza, m'dziko lonse la Ejipito. Ndipo anatenga phulusa la m'ng'anjo, naima pamaso pa Farao; ndi Mose analiwaza kuthambo; ndipo linakhala zilonda zobuka ndi matuza pa anthu ndi pa zoweta. Ndipo alembi sanakhoza kuima pamaso pa Mose chifukwa cha zilondazo; popeza panali zilonda pa alembi ndi pa Aejipito onse. Koma Yehova analimbitsa mtima wa Farao, kuti sanamvere iwo; monga Yehova adalankhula ndi Mose. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Uka nulawire mamawa, nuime pamaso pa Farao, nunene naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Lola anthu anga amuke, akanditumikire. Pakuti nthawi yino ndidzatuma miliri yanga yonse pamtima pako, ndi pa anyamata ako, ndi pa anthu ako; kuti udziwe kuti palibe wina wonga Ine pa dziko lonse lapansi. Pakuti ndatambasula dzanja langa tsopano, kuti ndikupande iwe ndi anthu ako ndi mliri, ndi kuti uonongeke pa dziko lapansi. Koma ndithu chifukwa chake ndakuimika kuti ndikuonetse mphamvu yanga, ndi kuti alalikire dzina langa pa dziko lonse lapansi. Kodi udzikwezanso pa anthu anga, ndi kusawalola amuke? Taona, mawa monga nthawi yino ndidzavumbitsa mvumbi wa matalala, sipadakhala unzake m'Ejipito kuyambira tsiku lija lidakhazikika kufikira lero lino. Ndipo tsopano, tumiza, thawitsa zoweta zako ndi zonse uli nazo pabwalo; pakuti anthu onse ndi zoweta zonse zopezeka pabwalo, zosasonkhanidwa m'nyumba, matalala adzazigwera, ndipo zidzafa. Iyeyu wa anyamata a Farao wakuopa mau a Yehova anathawitsira m'zinyumba anyamata ake ndi zoweta zake; koma iyeyu wosasamalira mau a Yehova anasiya anyamata ndi zoweta zake kubusa. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasula dzanja lako kuthambo, kuti pakhale matalala pa dziko lonse la Ejipito, pa anthu ndi pa zoweta, ndi pa zitsamba zonse za kuthengo, m'dziko la Ejipito. Pamenepo Mose anasamulira ndodo yake kuthambo, ndipo Yehova anatumiza bingu ndi matalala, ndi moto unatsikira pansi; ndipo Yehova anavumbitsa matalala pa dziko la Ejipito. Potero panali matalala, ndi moto wakutsikatsika pakati pa matalala, choopsa ndithu; panalibe chotere m'dziko lonse la Ejipito chiyambire mtundu wao. Ndipo matalala anapanda m'dziko lonse la Ejipito zonse za pabwalo, kuyambira anthu kufikira zoweta; ndipo matalala anapanda zitsamba zonse za kuthengo, nathyola mitengo yonse ya kuthengo. M'dziko la Goseni mokha, mokhala ana a Israele, munalibe matalala. Ndipo Farao anatumiza, naitana Mose ndi Aroni, nanena nao, Ndachimwa tsopano; Yehova ndiye wolungama, ine ndi anthu anga ndife oipa. Pembani kwa Yehova; chifukwa akwanira ndithu mabingu a Mulungu ndi matalala; ndipo ndidzakulolani mumuke, osakhalanso. Ndipo Mose ananena naye, Potuluka m'mudzi ine, ndidzasasatulira manja anga kwa Yehova; mabingu adzaleka, ndi matalala sadzakhalaponso; kuti mudziwe kuti dziko lapansi nla Yehova. Koma inu ndi anyamata anu ndidziwa kuti simudzayamba kuopa nkhope ya Yehova Mulungu. Ndipo thonje ndi barele zinayoyoka; pakuti barele lidafula, ndi thonje lidayamba maluwa. Koma tirigu ndi rai sizinayoyoka popeza amabzala m'mbuyo. Ndipo Mose anatuluka kwa Farao m'mudzi nasasatulira manja ake kwa Yehova; ndipo mabingu ndi matalala analeka, ndi mvula siinavumbanso padziko. Pamene Farao anaona kuti mvula ndi matalala ndi mabingu zidaleka anaonjezanso kuchimwa, naumitsa mtima wake, iye ndi anyamata ake. Potero mtima wa Farao unalimba, ndipo sanalole ana a Israele amuke; monga Yehova adalankhula mwa Mose. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lowa kwa Farao; pakuti ndaumitsa mtima wake, ndi mtima wa anyamata ake, kuti ndiike zizindikiro zanga izi pakati pao; ndi kuti ufotokozere m'makutu a ana ako, ndi a zidzukulu zako, chomwe ndidzachita m'Ejipito, ndi zizindikiro zanga zimene ndinaziika pakati pao; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova. Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao nanena naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Ukana kudzichepetsa pamaso panga kufikira liti? Lola anthu anga amuke, akanditumikire; pakuti ukakana kulola anthu anga amuke, taona, mawa ndidzafikitsa dzombe m'dziko lako; ndipo lidzakuta nkhope ya dziko, kotero kuti palibe munthu adzakhoza kuona dziko; ndipo lidzadya zotsalira zidapulumuka, zidatsalira inu pamatalala, ndipo lidzadya mtengo uliwonse wokuphukirani kuthengo; ndipo lidzadzaza m'nyumba zako, ndi m'nyumba za anyamata ako onse, ndi m'nyumba za Aejipito onse; sanachione chotere atate ako kapena makolo ako, kuyambira tsiku lija lakukhala iwo pa dziko lapansi kufikira lero lino. Ndipo anatembenuka, natuluka kwa Farao. Ndipo anyamata ake a Farao ananena naye, Ameneyo amatichitira msampha kufikira liti? Lolani anthuwo amuke, akatumikire Yehova Mulungu wao. Kodi simunayambe kudziwa kuti Ejipito laonongeka? Ndipo anawabwereretsa Mose ndi Aroni kwa Farao, nanena nao, Mukani, katumikireni Yehova Mulungu wanu. Koma amene adzapitawo ndiwo yani? Ndipo Mose anati, Tidzamuka ndi ana athu ndi akulu athu, ndi ana athu aamuna ndi aakazi; tidzamuka nazo nkhosa zathu ndi ng'ombe zathu; pakuti tili nao madyerero a Yehova. Ndipo ananena nao, Momwemo, Yehova akhale nanu ngati ndilola inu ndi ana ang'ono anu mumuke; chenjerani pakuti pali choipa pamaso panu. Chotero ai, mukani tsopano, inu amuna akulu, tumikirani Yehova pakuti ichi muchifuna. Ndipo anawapirikitsa pamaso pa Farao. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako pa dziko la Ejipito, lidze dzombe, kuti likwere pa dziko la Ejipito, lidye zitsamba zonse za m'dziko, ndizo zonse adazisiya matalala. Pamenepo Mose analoza ndodo yake pa dziko la Ejipito; ndipo Yehova anaombetsa padziko mphepo ya kum'mawa usana wonse, ndi usiku womwe; ndipo kutacha mphepo ya kum'mawa inadza nalo dzombe. Ndipo dzombe linakwera pa dziko lonse la Ejipito, ndipo linatera pakati pa malire onse Ejipito, lambirimbiri; lisanafike ili panalibe dzombe lotere longa ili, ndipo litapita ili sipadzakhalanso lotere. Pakuti linakuta nkhope ya dziko lonse kuti dziko linada; ndipo linadya zitsamba zonse za m'dziko, ndi zipatso zonse za mitengo zimene matalala adazisiya; ndipo sipanatsala chabiriwiri chilichonse, pamitengo kapena pa zitsamba za kuthengo, m'dziko lonse la Ejipito. Pamenepo Farao anafulumira kuitana Mose ndi Aroni; nati, Ndalakwira Yehova Mulungu wanu, ndi inu. Ndipo tsopano, ndikhululukiretu kulakwa kwanga nthawi yino yokha, nimundipembere kwa Yehova Mulungu wanu, kuti andichotsere imfa yino yokha. Ndipo anatuluka kwa Farao, napemba Yehova. Ndipo Yehova anabweza mphepo yolimbatu ya kumadzulo, imene inapita nalo dzombe niliponya m'Nyanja Yofiira: silinatsala dzombe limodzi pakati pa malire onse a Ejipito. Koma Yehova analimbitsa mtima wa Farao, ndipo sanalole ana a Israele amuke. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako kuthambo, ndipo padzakhala mdima pa dziko la Ejipito, ndiwo mdima wokhudzika. Ndipo Mose anatambasulira dzanja lake kuthambo; ndipo munali mdima bii m'dziko lonse la Ejipito masiku atatu; sanaonane, sanaukenso munthu pamalo pake, masiku atatu; koma kwa ana onse a Israele kudayera m'nyumba zao. Ndipo Farao anaitana Mose, nati, Mukani, tumikirani Yehova; nkhosa zanu ndi ng'ombe zanu zokha zitsale; mumuke nao ana anu ang'ononso. Koma Mose anati, Mutipatsenso m'dzanja mwathu nsembe zophera ndi nsembe zopsereza, kuti timkonzere Yehova Mulungu wathu. Zoweta zathu zomwe tidzapita nazo; chosatsala chiboda chimodzi; pakuti mwa izo tiyenera kutenga zakutumikira nazo Yehova Mulungu wathu; ndipo tisanafikeko, sitidziwa umo tidzamtumikira Yehova. Koma Yehova analimbitsa mtima wake wa Farao, ndipo anakana kuwaleka amuke. Ndipo Farao ananena naye, Choka pano, uzichenjera usaonenso nkhope yanga; pakuti tsiku limene uonanso nkhope yanga udzafa. Ndipo Mose anati, Mwanena bwino; sindidzaonanso nkhope yanu. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Watsala mliri umodzi ndidzamtengera Farao, ndi Ejipito; pambuyo pake adzakulolani muchoke kuno; pamene akulolani kupita, zoonadi adzakuingitsani kuno konse. Lankhula tsopano m'makutu a anthu, kuti mwamuna yense apemphe kwa mnzake, ndi mkazi yense kwa mnzake, zokometsera zasiliva ndi zagolide. Ndipo Yehova anawapatsa anthu chisomo pamaso pa Aejipito. Munthuyo Mose ndiyenso wamkulu ndithu m'dziko la Ejipito, pamaso pa anyamata a Farao, ndi pamaso pa anthu. Ndipo Mose anati, Atero Yehova, Monga pakati pa usiku ndidzatuluka Ine kunka pakati pa Aejipito; ndipo ana oyamba a m'dziko la Ejipito adzafa, kuyambira mwana woyamba wa Farao wokhala pa mpando wachifumu wake, kufikira mwana woyamba wa mdzakazi wokhala pa miyala yopera; ndi ana onse oyamba a zoweta. Ndipo kudzakhala kulira kwakukulu m'dziko lonse la Ejipito, kunalibe kunzake kotere, sikudzakhalanso kunzake kotere. Koma palibe galu adzafunyitsira lilime lake ana onse a Israele ngakhale anthu kapena zoweta; kuti mudziwe kuti Yehova asiyanitsa pakati pa Aejipito ndi Aisraele. Ndipo anyamata ako onse awa adzanditsikira, nadzandigwadira, ndi kuti, Tulukani inu, ndi anthu onse akukutsatani; ndipo pambuyo pake ndidzatuluka. Ndipo anatuluka kwa Farao wakupsa mtima. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Farao sadzamvera inu; kuti zozizwa zanga zichuluke m'dziko la Ejipito. Ndipo Mose ndi Aroni anachita zozizwa izi zonse pamaso pa Farao; koma Yehova analimbitsa mtima wake wa Farao, ndipo sanalole ana a Israele atuluke m'dziko lake. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni m'dziko la Ejipito, ndi kuti, Mwezi uno uzikhala kwa inu woyamba wa miyezi; muziuyesa mwezi woyamba wa chaka. Mulankhule ndi msonkhano wonse wa Israele ndi kuti, Tsiku lakhumi la mwezi uno adzitengere munthu yense mwanawankhosa, monga mwa mabanja a atate ao, mwanawankhosa pabanja. Banja likaperewera mwanawankhosa, munthu ndi mnzake ali pafupi pa nyumba yake atenge monga mwa kufikira kwa anthu ao; muziwerengera mwanawankhosa monga mwa kudya kwao. Mwanawankhosa wanu azikhala wangwiro, wamwamuna, wa chaka chimodzi; muzimtenga ku nkhosa kapena ku mbuzi. Ndipo mukhale naye chisungire kufikira tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi womwe; ndipo bungwe lonse la anthu a Israele lizimupha madzulo. Ndipo azitengako mwazi, naupake pa mphuthu za mbali ndi ya pamwamba m'nyumba zimene adyeramo. Ndipo azidya nyamayo usiku womwewo, yoocha pamoto, ndi mkate wopanda chotupitsa; aidye ndi ndiwo zowawa. Musaidya yaiwisi, kapena yophika ndi madzi konse ai, koma yoocha pamoto; mutu wake ndi miyendo yake ndi matumbo ake. Ndipo musasiyako kufikira m'mawa; koma yotsalira kufikira m'mamawayo muipsereze ndi moto. Ndipo muziidya chotero: okwinda m'chuuno, nsapato zanu pa mapazi anu ndodo yanu m'dzanja lanu, ndipo muziidya msanga; ndiye Paska wa Yehova. Pakuti ndidzapita pakati pa dziko la Ejipito usiku womwewo, ndi kukantha ana oyamba onse m'dziko la Ejipito, anthu ndi zoweta; ndipo ndidzachita maweruzo pa milungu yonse ya Aejipito; Ine ndine Yehova. Ndipo mwaziwo udzakhala chizindikiro kwa inu pa nyumba zimene mukhalamo; pamene ndiona mwaziwo ndidzapitirira inu, ndipo sipadzakhala mliri wakukuonongani, pakukantha Ine dziko la Ejipito. Ndipo tsiku lino lidzakhala kwa inu chikumbutso, muzilisunga la chikondwerero cha Yehova; ku mibadwo yanu muzilisunga la chikondwerero, likhale lemba losatha. Masiku asanu ndi awiri muzidya mkate wopanda chotupitsa; lingakhale tsiku loyamba muzichotsa chotupitsa m'nyumba zanu; pakuti aliyense wakudya mkate wa chotupitsa kuyambira tsiku loyamba kufikira tsiku lachisanu ndi chiwiri, munthu amene adzasadzidwa kwa Israele. Ndipo tsiku loyamba kukhale kusonkhana kopatulika, ndi tsiku lachisanu ndi chiwiri kukhalenso kusonkhana kopatulika; pasachitike ntchito masikuwo, zokhazi zakudya anthu onse ndizo muzichita. Ndipo muzisunga chikondwerero a Mkate wopanda chotupitsa; pakuti tsiku lomwe lino ndinatulutsa makamu anu m'dziko la Ejipito; chifukwa chake muzisunga tsiku lino m'mibadwo yanu, lemba losatha. Mwezi woyamba, tsiku lake lakhumi ndi chinai madzulo ake, muzidya mkate wopanda chotupitsa, kufikira tsiku la makumi awiri mphambu limodzi la mwezi, madzulo ake. Chisapezeke chotupitsa m'nyumba zanu masiku asanu ndi awiri; pakuti aliyense wakudya kanthu ka chotupitsa, munthuyo adzasadzidwa ku msonkhano wa Israele, angakhale ndiye mlendo kapena wobadwa m'dziko. Musadye kanthu ka chotupitsa; mokhala inu monse muzidya mkate wopanda chotupitsa. Pamenepo Mose anaitana akulu onse a Israele, nanena nao, Pitani, dzitengereni anaankhosa monga mwa mabanja anu, nimuphere Paska. Ndipo muzitenga mpukutu wa hisope, ndi kuuviika m'mwazi uli m'mbale, ndi kupaka mwazi uli m'mbalemo pa mphuthu ya pamwamba ndi pambali; koma inu, asatuluke munthu pakhomo pa nyumba yake kufikira m'mawa. Pakuti Yehova adzapita pakatipo kukantha Aejipito; koma pamene adzaona mwaziwo pa mphuthu pamwamba ndi za pambali, Yehova adzapitirira pakhomopo, osalola woononga alowe m'nyumba zanu kukukanthani. Ndipo muzisunga chinthu ichi chikhale lemba la kwa inu, ndi kwa ana anu ku nthawi zonse. Ndipo kudzakhala, pamene mulowa m'dziko limene Yehova adzakupatsani, monga analankhula, muzisunga kutumikira kumeneku. Ndipo kudzakhala, pamene ana anu adzanena ndi inu, Kutumikiraku muli nako nkutani? Mudzati, Ndiko nsembe ya Paska wa Yehova, amene anapitirira nyumba za ana a Israele m'Ejipito, pamene anakantha Aejipito, napulumutsa nyumba zathu. Ndipo anthu anawerama, nalambira. Ndipo ana a Israele anamuka nachita monga Yehova adalamulira Mose ndi Aroni; anachita momwemo. Ndipo panakhala pakati pa usiku, Yehova anakantha ana oyamba onse a m'dziko la Ejipito, kuyambira mwana woyamba wa Farao wakukhala pa mpando wachifumu wake kufikira mwana woyamba wa wam'nsinga ali m'kaidi; ndi ana oyamba onse a zoweta. Ndipo Farao anauka usiku, iye ndi anyamata ake onse ndi Aejipito onse; ndipo kunali kulira kwakukulu m'Ejipito; pakuti panalibe nyumba yopanda wakufa m'mwemo. Ndipo anaitana Mose ndi Aroni usiku, nati, Ukani, tulukani pakati pa anthu anga, inu ndi ana a Israele; ndipo mukani katumikireni Yehova, monga mwanena. Muka nazoni zoweta zanu zazing'ono ndi zazikulu, monga mwanena; chokani, ndi kundidalitsa inenso. Ndipo Aejipito anaumiriza anthuwo, nafulumira kuwatulutsa m'dziko; pakuti anati, Tili akufa tonse. Ndipo anthu anatenga mtanda wao usanatupe, ndi zoumbiramo zao zomangidwa m'zovala zao pa mapewa ao. Ndipo ana a Israele anachita monga mwa mau a Mose; napempha Aejipito zokometsera zasiliva, ndi zagolide, ndi zovala. Ndipo Yehova anapatsa anthu chisomo pamaso pa Aejipito, ndipo sanawakanize. Ndipo anawafunkhira Aejipito. Ndipo ana a Israele anayenda ulendo wakuchokera ku Ramsesi kufikira ku Sukoti, zikwi mazana asanu ndi limodzi oyenda okha, ndiwo amuna, osawerenga ana. Ndipo anthu ambiri osokonezeka anakwera nao; ndi nkhosa ndi ng'ombe, zoweta zambirimbiri. Ndipo anaotcha timitanda topanda chotupitsa ta mtanda umene anabwera nao ku Ejipito, popeza sadaikamo chotupitsa; pakuti adawapirikitsa ku Ejipito, ndipo sanathe kuchedwa, kapena kudzikonzeratu kamba. Ndipo kukhala kwa ana a Israele anakhala m'Ejipito ndiko zaka mazana anai kudza makumi atatu. Ndipo kunakhala pakutha zaka mazana anai kudza makumi atatu, inde panakhala tsiku lomwelo, makamu onse a Yehova anatuluka m'dziko la Ejipito. Ndiwo usiku wosungira Yehova ndithu, chifukwa cha kuwatulutsa m'dziko la Ejipito; usiku womwe uno ukhale wosungira Yehova ana onse a Israele ku mibadwo yao. Ndipo Yehova anati kwa Mose ndi Aroni, Lemba la Paska ndi ili: mwana wa mlendo aliyense asadyeko; koma kapolo wa mwini aliyense, wogula ndi ndalama, utamdula, ndipo adyeko. Mlendo kapena wolembedwa ntchito asadyeko. Audye m'nyumba imodzi; usatulukira nayo kubwalo nyama ina; ndipo musathyole fupa lake. Msonkhano wonse wa Israele uzichita ichi. Koma akakhala nanu mlendo, nakonzera Yehova Paska, adulidwe amuna ake onse, ndipo pamenepo asendere kuuchita; nakhale ngati wobadwa m'dziko; koma wosadulidwa aliyense asadyeko. Pakhale lamulo lomweli pa wobadwa m'dziko, ndi pa mlendo wakukhala pakati pa inu. Ndipo ana onse a Israele anachita monga Yehova adawalamulira Mose ndi Aroni, momwemo anachita. Ndipo kunakhala tsiku lomwelo, kuti Yehova anatulutsa ana a Israele m'dziko la Ejipito, monga mwa makamu ao. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi kuti, Ndipatulire Ine yense woyamba kubadwa, wotsegulira pa amake mwa ana a Israele, mwa anthu ndi mwa zoweta; ndiwo anga. Ndipo Mose ananena ndi anthu, Kumbukirani tsiku lino limene munatuluka m'Ejipito, m'nyumba ya akapolo; pakuti Yehova anakutulutsani muno ndi dzanja lamphamvu; ndipo asadye kanthu ka chotupitsa. Mutuluka lero lino mwezi wa Abibu. Ndipo kudzakhala atakulowetsa Yehova m'dziko la Akanani, ndi la Ahiti, ndi la Aamori ndi la Ahivi, ndi la Ayebusi, limene analumbira ndi makolo ako kukupatsa, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, uzikasunga kutumikira kumeneku mwezi uno. Masiku asanu ndi awiri uzikadya mkate wopanda chotupitsa, ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri likhale la madyerero a Yehova; Azikadya mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiriwo ndipo kasaoneke kanthu ka chotupitsa kwanu; inde chotupitsa chisaoneke kwanu m'malire ako onse. Ndipo ukauze mwana wako wamwamuna tsikulo, ndi kuti, Nditero chifukwa chomwe Yehova anandichitira ine potuluka ine m'Ejipito. Ndipo chizikhala ndi iwe ngati chizindikiro pa dzanja lako, ndi chikumbutso pakati pa maso ako; kuti chilamulo cha Yehova chikhale m'kamwa mwako; pakuti Yehova anakutulutsa m'Ejipito ndi dzanja lamphamvu. Chifukwa chake uzikasunga lemba ili pa nyengo yake chaka ndi chaka. Ndipo kudzakhala, atakulowetsa Yehova m'dziko la Akanani, monga anakulumbirira iwe ndi makolo ako, ndipo anakupatsa ilo, kuti uzikapatulira Yehova onse oyamba kubadwa ndi oyamba onse uli nao odzera kwa zoweta; amunawo ndi a Yehova. Koma woyamba yense wa bulu uzimuombola ndi mwanawankhosa; ndipo ukapanda kumuombola uzimthyola khosi; koma oyamba onse a munthu mwa ana ako uziwaombola. Ndipo kudzakhala, akakufunsa mwana wako masiku akudzawo ndi kuti, Ichi nchiyani? Ukanene naye, Yehova anatitulutsa m'Ejipito, m'nyumba ya akapolo, ndi dzanja lamphamvu; ndipo kunakhala, pamene Farao anadziumitsa kuti tisamuke, Yehova anawapha onse oyamba kubadwa m'dziko la Ejipito, kuyambira oyamba a anthu, kufikira oyamba a zoweta; chifukwa chake ndimphera nsembe Yehova zazimuna zoyamba kubadwa zonse; koma oyamba onse a ana anga ndiwaombola. Ndipo chizikhala ngati chizindikiro pa dzanja lako, ndi chapamphumi pakati pa maso ako; pakuti Yehova anatitulutsa m'Ejipito ndi dzanja lamphamvu. Ndipo kunakhala pamene Farao adalola anthu amuke, Mulungu sanawatsogolere njira ya dziko la Afilisti, ndiyo yaifupi; pakuti Mulungu anati, Angadodome anthuwo pakuona nkhondo ndi kubwerera m'mbuyo kunka ku Ejipito. Koma Mulungu anawazungulitsa anthuwo, ku njira ya kuchipululu ya Nyanja Yofiira; ndipo ana a Israele anakwera kuchokera m'dziko la Ejipito okonzeka. Ndipo Mose anamuka nao mafupa a Yosefe; pakuti adawalumbiritsatu ana a Israele ndi kuti, Mulungu adzakuzondani ndithu ndipo mukakwere nao mafupa anga osawasiya kuno. Ndipo anachokera ku Sukoti, nagona ku Etamu, pa malekezero a chipululu. Ndipo Yehova anawatsogolera usana ndi mtambo njo kuwatsogolera m'njira; ndi usiku ndi moto njo, wakuwawalitsira; kuti ayende usana ndi usiku; sanachotse mtambo usana, kapena mtambo wamoto usiku, pamaso pa anthu. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi kuti, Lankhula ndi anthu a Israele, kuti abwerere m'mbuyo nagone patsogolo pa Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja, patsogolo pa Baala-Zefoni; pandunji pake mugone panyanja. Ndipo Farao adzanena za ana a Israele, Azimidwa dziko, chipululu chawatsekera. Ndipo ndidzalimbitsa mtima wake wa Farao kuti awalondole; ndipo ndidzalemekezedwa pa Farao ndi pa nkhondo yake yonse; pamenepo Aejipito adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndipo anachita chomwecho. Ndipo anauza mfumu ya Aejipito kuti anthu adathawa; ndi mtima wa Farao ndi wa anyamata ake inasandulikira anthuwo, ndipo anati, Ichi nchiyani tachita, kuti talola Israele amuke osatigwiriranso ntchito? Ndipo anamanga galeta lake, napita nao anthu ake; napita nao magaleta osankhika mazana asanu ndi limodzi, ndi magaleta onse a m'Ejipito, ndi akapitao ao onse. Ndipo Yehova analimbitsa mtima wa Farao, mfumu ya Aejipito, ndipo iye analondola ana a Israele; koma ana a Israele adatuluka ndi dzanja lokwezeka. Ndipo Aejipito anawalondola, ndiwo akavalo ndi magaleta onse a Farao, ndi apakavalo ake, ndi nkhondo yake, nawapeza ali kuchigono kunyanja, pa Pihahiroti, patsogolo pa Baala-Zefoni. Ndipo pamene Farao anayandikira ana a Israele anatukula maso ao, taonani, Aejipito alinkutsata pambuyo pao; ndipo anaopa kwambiri; ndi ana a Israele anafuulira kwa Yehova. Ndipo anati kwa Mose, Kodi mwatichotsera kuti tikafe m'chipululu chifukwa panalibe manda m'Ejipito? Nchiyani ichi mwatichitira kuti mwatitulutsa m'Ejipito? Si awa mauwo tinalankhula nanu m'Ejipito ndi kuti, Tilekeni, kuti tigwirire ntchito Aejipito? Pakuti kutumikira Aejipito kutikomera si kufa m'chipululu ai. Ndipo Mose ananena ndi anthu, Musaope, chilimikani, ndipo penyani chipulumutso cha Yehova, chimene adzakuchitirani lero; pakuti Aejipito mwawaona lerowa, simudzawaonanso konse. Yehova adzakugwirirani nkhondo, ndipo inu mudzakhala chete. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ufuuliranji kwa Ine? Lankhula ndi ana a Israele kuti aziyenda. Ndipo iwe nyamula ndodo yako, nutambasulire dzanja lako kunyanja, nuigawe, kuti ana a Israele alowe pakati pa nyanja pouma. Ndipo Ine, taonani, ndidzalimbitsa mitima ya Aejipito, kuti alowemo powatsata; ndipo ndidzalemekezedwa pa Farao, ndi pa nkhondo yake yonse, pa magaleta ake, ndi pa okwera pa akavalo ake. Ndipo Aejipito adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, polemekezedwa Ine pa Farao, pa magaleta ake, ndi pa okwera pa akavalo ake. Ndipo mthenga wa Mulungu, wakutsogolera ulendo wa Israele, unachokako, nutsata pambuyo pao; ndipo mtambo njo uja unachoka patsogolo pao, nuima pambuyo pao; nulowa pakati pa ulendo wa Aejipito ndi ulendo wa Aisraele; ndipo mtambo unachita mdima, komanso unaunikira usiku; ndipo ulendo wina sunayandikizana ndi unzake usiku wonse. Ndipo Mose anatambasulira dzanja lake kunyanja; ndipo Yehova anabweza nyanja ndi mphepo yolimba ya kum'mawa usiku wonse, naumitsa nyanja; ndipo madziwo anagawikana. Ndipo ana a Israele analowa pakati pa nyanja pouma; ndi madziwo anakhala kwa iwo ngati khoma palamanja, ndi palamanzere. Ndipo Aejipito anawalondola, nalowa pakati pa nyanja powatsata, ndiwo akavalo onse a Farao, magaleta ake, ndi apakavalo ake. Ndipo kunali, ulonda wa mamawa, Yehova ali m'moto ndi m'mtambo njo anapenyera pa ulendo wa Aejipito, nauvuta ulendo wa Aejipito. Ndipo anagulula njinga za magaleta ao, nawayendetsa molemetsa; pamenepo Aejipito anati, Tithawe pamaso pa Israele; pakuti Yehova alikuwagwirira nkhondo pa Aejipito. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako kunyanja, kuti madziwo abwerere kudzamiza Aejipito, magaleta ao, ndi apakavalo ao. Ndipo Mose anatambasulira dzanja lake kunyanja, ndi nyanja inabwerera m'mayendedwe ake mbandakucha; ndipo Aejipito pothawa anakomana nayo; ndipo Yehova anakutumula Aejipito m'kati mwa nyanja. Popeza madziwo anabwerera, namiza magaleta ndi apakavalo, ndiwo nkhondo yonse ya Farao imene idalowa pambuyo pao m'nyanja; sanatsale wa iwowa ndi mmodzi yense. Koma ana a Israele anayenda pouma pakati pa nyanja; ndi madziwo anakhala ngati khoma kwa iwo, palamanja ndi lamanzere. Chomwecho Yehova anapulumutsa Israele tsiku lomwelo m'manja a Aejipito; ndipo Israele anaona Aejipito akufa m'mphepete mwa nyanja. Ndipo Israele anaiona ntchito yaikulu imene Yehova anachitira Aejipito, ndipo anthuwo anaopa Yehova; nakhulupirira Yehova ndi mtumiki wake Mose. Pamenepo Mose ndi ana a Israele anaimbira Yehova nyimbo iyi, nanena, ndi kuti, Ndidzaimbira Yehova pakuti wapambanatu; kavalo ndi wokwera wake anawaponya m'nyanja. Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, ndipo wakhala chipulumutso changa; ameneyo ndiye Mulungu wanga, ndidzamlemekeza; ndiye Mulungu wa kholo langa, ndidzamveketsa. Yehova ndiye wankhondo; dzina lake ndiye Yehova. Magaleta a Farao ndi nkhondo yake anawaponya m'nyanja; ndi akazembe ake osankhika anamira m'Nyanja Yofiira. Nyanja inawamiza; anamira mozama ngati mwala. Dzanja lanu lamanja, Yehova, lalemekezedwa ndi mphamvu, dzanja lanu lamanja, Yehova, laphwanya mdani. Ndipo ndi ukulu wanu waukulu mwapasula akuukira Inu; mwatumiza mkwiyo wanu, unawanyeketsa ngati chiputu. Ndipo ndi mpumo wa m'mphuno mwanu madzi anaunjikika, mayendedwe ake anakhala chilili ngati mulu; zozama zinalimba m'kati mwa nyanja. Mdani anati, Ndiwalondola, ndiwapeza, ndidzagawa zofunkha; ndidzakhuta nao mtima; ndidzasolola lupanga langa, dzanja langa lidzawaononga. Munaombetsa mphepo yanu, nyanja inawamiza; anamira m'madzi aakulu ngati mtovu. Afanana ndi Inu ndani mwa milungu, Yehova? Afanana ndi Inu ndani, wolemekezedwa, woyera, woopsa pomyamika, wakuchita zozizwa? Mwatambasula dzanja lanu lamanja, nthaka inawameza. Mwa chifundo chanu mwatsogolera anthu amene mudawaombola; mwamphamvu yanu mudawalondolera njira yakunka pokhala panu poyera. Mitundu ya anthu idamva, inanthunthumira; kuda mtima kwagwira anthu okhala m'Filistiya. Pamenepo mafumu a Edomu anadabwa; agwidwa nako kunthunthumira amphamvu a ku Mowabu; okhala m'Kanani onse asungunuka mtima. Kuopa kwakukulu ndi mantha ziwagwera; pa dzanja lanu lalikulu akhala chete ngati mwala; kufikira apita anthu anu, Yehova, kufikira apita anthu amene mudawaombola. Mudzawafikitsa, ndi kuwaoka pa phiri la cholowa chanu, pamalo pamene munadzipangira mukhalepo, Yehova, malo oyera, amene manja anu, Ambuye, adakhazikika. Yehova adzachita ufumu nthawi yonka muyaya. Pakuti akavalo a Farao analowa m'nyanja, ndi magaleta ake ndi apakavalo ake, ndipo Yehova anawabwezera madzi a m'nyanja; koma ana a Israele anayenda pouma pakati pa nyanja. Ndipo Miriyamu mneneriyo, mlongo wa Aroni, anagwira lingaka m'dzanja lake; ndipo akazi onse anatuluka kumtsata ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe. Ndipo Miriyamu anawayankha, Imbirani Yehova, pakuti wapambanatu; kavalo ndi wokwera wake anawaponya m'nyanja. Ndipo Mose anatsogolera Israele kuchokera ku Nyanja Yofiira, ndipo anatulukako nalowa m'chipululu cha Suri; nayenda m'chipululu masiku atatu, osapeza madzi. Pamene anafika ku Mara sanakhoze kumwa madzi a Mara, pakuti anali owawa; chifukwa chake anatcha dzina lake Mara. Ndipo anthu anadandaulira Mose, ndi kuti, Tidzamwa chiyani? Ndipo iye anafuulira kwa Yehova; ndipo Yehova anamsonyeza mtengo ndipo anauponya m'madzimo, ndi madzi anasanduka okoma. Pamenepo anawapangira lemba ndi chiweruzo, ndi pomwepa anawayesa; ndipo anati, Ngati udzamveratu mau a Yehova, Mulungu wako, ndi kuchita zoona pamaso pake, ndi kutchera khutu pa malamulo ake, ndi kusunga malemba ake onse, za nthenda zonse ndinaziika pa Aejipito sindidzaziika pa iwe nnena imodzi; pakuti Ine Yehova ndine wakuchiritsa iwe. Ndipo anafika pa Elimu, ndi pamenepo panali akasupe a madzi khumi ndi awiri, ndi akanjedza makumi asanu ndi awiri; ndipo anamanga chigono chao pomwepo pa madziwo. Ndipo anachoka ku Elimu, ndi khamu lonse la ana a Israele linalowa m'chipululu cha Sini, ndicho pakati pa Elimu ndi Sinai, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachiwiri atatuluka m'dziko la Ejipito. Ndipo khamu lonse la ana a Israele linadandaulira Mose ndi Aroni m'chipululu nanena nao ana a Israele, Ha? Mwenzi titafa ndi dzanja la Yehova m'dziko la Ejipito, pokhala ife pa miphika ya nyama, pakudya mkate ife chokhuta; pakuti mwatitulutsa kudza nafe m'chipululu muno kudzapha msonkhano uwu wonse ndi njala. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndidzavumbitsira inu mkate wodzera kumwamba; ndipo anthu azituluka ndi kuola muyeso wa tsiku pa tsiku lake, kuti ndiwayese, ngati ayenda m'chilamulo changa kapena iai. Ndipo kudzakhala tsiku lachisanu ndi chimodzi, kuti azikonza umene adabwera nao, ataonjezapo muyeso unzake wa pa tsiku limodzi. Ndipo Mose ndi Aroni ananena ndi ana onse a Israele, Madzulo mudzadziwa kuti Yehova anakutulutsani m'dziko la Ejipito; ndi m'mawa mwake mudzaona ulemerero wa Yehova, popeza alinkumva mulikudandaulira Yehova; pakuti ife ndife chiyani, kuti mutidandaulira ife? Nanenanso Mose, Pakukupatsani Yehova nyama ya kudya madzulo, ndi mkate wokhuta m'mawa, atero popeza Yehova adamva madandaulo anu amene mumdandaulira nao. Koma ife ndife chiyani? Simulikudandaulira ife koma Yehova. Ndipo Mose anati kwa Aroni, Nena ndi khamu lonse la ana a Israele, Yandikizani pamaso pa Yehova, pakuti anamva madandaulo anu. Ndipo kunakhala, pakunena Aroni ndi khamu lonse la ana a Israele kuti iwo anatembenukira kuchipululu, ndipo, taonani, ulemerero wa Yehova unaoneka mumtambo. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Ndamva madandaulo a ana a Israele; lankhula nao ndi kuti, Madzulo mudzadya nyama, ndi m'mawa mudzakhuta mkate; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu. Ndipo kunali madzulo zinakwera zinziri, ndipo zinakuta tsasa, ndi m'mawa padagwa mame pozungulira tsasa. Ndipo atasansuka mame adagwawo, taonani, pankhope pa chipululu pali kanthu kakang'ono kamphumphu, kakang'ono ngati chipale panthaka. Ndipo pamene ana a Israele anakaona, anati wina ndi mnzake, Nchiyani ichi? Pakuti sanadziwe ngati nchiyani. Ndipo Mose ananena nao, Ndiwo mkatewo Yehova wakupatsani ukhale chakudya chanu. Amenewo ndiwo mau walamulira Yehova, Aoleko yense monga mwa njala yake; munthu mmodzi omeri limodzi, monga momwe muli, yense atengere iwo m'hema mwake. Ndipo ana a Israele anatero, naola wina wambiri, wina pang'ono. Ndipo pamene anayesa ndi omeri, iye amene adaola wambiri sunamtsalira, ndi iye amene adaola pang'ono sunamsowa; yense anaola monga mwa njala yake. Ndipo Mose ananena nao, Palibe munthu asiyeko kufikira m'mawa. Koma sanammvere Mose; ndipo ena anasiyako kufikira m'mawa; koma unagwa mphutsi, nununkha. Ndipo Mose anakwiya nao. Ndipo anauola m'mawa ndi m'mawa, yense monga mwa njala yake; popeza likatentha dzuwa umasungunuka. Ndipo kunali tsiku lachisanu ndi chimodzi, anaola mkate, naonjezapo linzake, maomeri awiri pa munthu mmodzi; ndipo akazembe a khamulo anadza nauza Mose. Ndipo ananena nao, Ichi ndi chomwe Yehova analankhula, Mawa ndiko kupuma, Sabata lopatulika la Yehova; chimene muziocha, ochani, ndi chimene muziphika phikani; ndi chotsala chikukhalireni chosungika kufikira m'mawa. Ndipo anausunga kufikira m'mawa, monga adalamulira Mose; koma sunanunkha, ndipo sunagwa mphutsi. Ndipo Mose anati, Muudye lero; pakuti lero ndilo Sabata la Yehova; simuupeza lero pabwalo. Muziola uwu masiku asanu ndi limodzi; koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo la Sabata, pamenepo padzakhala palibe. Ndipo kunali tsiku la Sabata, kuti anthu ena anatuluka kukaola, koma sanaupeze. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Mukana kusunga zouza zanga ndi malamulo anga kufikira liti? Taonani, popeza Yehova anakupatsani Sabata, chifukwa chake tsiku lachisanu ndi chimodzi alikupatsa inu mkate wofikira masiku awiri; khalani yense m'malo mwake munthu asatuluke m'malo mwake tsiku lachisanu ndi chiwiri. Ndipo anthu anapumula tsiku lachisanu ndi chiwiri. Ndipo mbumba ya Israele inautcha dzina lake Mana; ndiwo ngati zipatso zampasa, oyera; powalawa akunga timitanda tosanganiza ndi uchi. Ndipo Mose anati, Awa ndi mau anauza Yehova, Dzazani omeri nao, asungikire mibadwo yanu; kuti aone mkatewo ndinakudyetsani nao m'chipululu, muja ndinakutulutsani m'dziko la Ejipito. Ndipo Mose anati kwa Aroni, Tenga mphika, nuthiremo mana odzala omeri, nuuike pamaso pa Yehova, usungikire mibadwo yanu. Monga Yehova anauza Mose, momwemo Aroni anauika patsogolo pa Mboni, usungikeko. Ndipo ana a Israele anadya mana zaka makumi anai, kufikira atalowa dziko la midzi; anadya mana kufikira analowa malire a dziko la Kanani. Koma omeri ndilo limodzi la magawo khumi la efa. Ndipo khamu lonse la ana a Israele linachoka m'chipululu cha Sini, M'zigono zao, monga mwa mau a Yehova, nagona m'Refidimu. Koma kumeneko kunalibe madzi akumwa anthu. Pamenepo anthu anatsutsana ndi Mose, nati, Tipatseni madzi timwe. Koma Mose ananena nao, Mutsutsana nane bwanji? Muyeseranji Yehova? Ndipo pomwepo anthu anamva ludzu lokhumba madzi; ndi anthu anadandaulira Mose, nati, Munatikwezeranji kuchokera ku Ejipito, kudzatipha ife ndi ana athu ndi zoweta zathu ndi ludzu? Ndipo Mose anafuulira kwa Yehova, ndi kuti, Ndiwachitenji anthuwa? Andilekera pang'ono kundiponya miyala. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Pita pamaso pa anthu, nutenge pamodzi nawe akulu ena a Israele; nutenge m'dzanja mwako ndodo ija unapanda nayo nyanja, numuke. Taona, ndidzaima pamaso pako pathanthwe m'Horebu; ndipo upande thanthwe, nadzatulukamo madzi, kuti anthu amwe. Ndipo Mose anachita chomwecho pamaso pa akulu a Israele. Ndipo anatcha dzina la malowo Masa, ndi Meriba, chifukwa cha kutsutsana kwa ana a Israele; popezanso anayesa Yehova, ndi kuti, Kodi Yehova ali pakati pa ife, kapena iai? Pamenepo anadza Amaleke, nayambana ndi Israele m'Refidimu. Ndipo Mose anati kwa Yoswa, Utisankhulire amuna, nutuluke kuyambana naye Amaleke; mawa ndidzaima pamwamba pa chitunda, ndi ndodo ya Mulungu m'dzanja langa. Ndipo Yoswa anachita monga Mose adanena naye, nayambana ndi Amaleke; ndipo Mose, ndi Aroni, ndi Huri anakwera pamwamba pa chitunda. Ndipo kunakhala, pamene Mose anakweza dzanja lake Israele analakika; koma pamene anatsitsa dzanja lake Amaleke analakika. Koma manja a Mose analema; ndipo anatenga mwala, nauika pansi pa iye, nakhala pamenepo; ndipo Aroni ndi Huri anagwiriziza manja ake, wina mbali ina, wina mbali ina; ndi manja ake analimbika kufikira litalowa dzuwa. Ndipo Yoswa anathyola Amaleke ndi anthu ake ndi ku ukali kwa lupanga. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lembera ichi m'buku, chikhale chikumbutso, nuchimvetse Yoswa; kuti ndidzafafaniza konse chikumbukiro cha Amaleke pansi pa thambo. Ndipo Mose anamanga guwa la nsembe, nalitcha dzina lake Yehova Nisi: nati, Yehova walumbira: padzakhala nkhondo ya Yehova pa Amaleke m'mibadwomibadwo. Ndipo Yetero, wansembe wa Midiyani, mpongozi wa Mose, anamva zonse zimene Mulungu adachitira Mose ndi Israele anthu ake, kuti Yehova adatulutsa Israele m'Ejipito. Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anabwera naye Zipora mkazi wa Mose (atamtuma kwao), ndi ana ake awiri; dzina la winayo ndiye Geresomo, pakuti anati, Ndakhala mlendo m'dziko lachilendo; ndi dzina la mnzake ndiye Eliyezere; pakuti anati, Mulungu wa kholo langa anakhala thandizo langa nandilanditsa ku lupanga la Farao. Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anadza ndi ana ake amuna ndi mkazi wake kwa Mose kuchipululu kumene adamangako, pa phiri la Mulungu; nati kwa Mose, Ine mpongozi wako Yetero ndadza kwa iwe, ndi mkazi wako, ndi ana ake omwe awiri. Ndipo Mose anatuluka kukakomana ndi mpongozi wake, nawerama, nampsompsona; nafunsana ali bwanji, nalowa m'hema. Ndipo Mose anafotokozera mpongozi wake zonse Yehova adazichitira Farao ndi Aejipito chifukwa cha Israele; ndi mavuto onse anakomana nao panjira, ndi kuti Yehova adawalanditsa. Ndipo Yetero anakondwera chifukwa cha zabwino zonse Yehova adazichitira Israele, ndi kuwalanditsa m'dzanja la Aejipito. Nati Yetero, Woyamikika Yehova, amene anakulanditsani m'dzanja la Aejipito, ndi m'dzanja la Farao; amene analanditsa anthu awa pansi pa dzanja la Aejipito. Tsopano ndidziwa kuti Yehova ali wamkulu ndi milungu yonse, pakuti momwe anadzikuza okha momwemo anawaposa. Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose, anamtengera Mulungu nsembe yopsereza, ndi nsembe zophera; ndipo Aroni ndi akulu onse a Israele anadza kudzadya mkate ndi mpongozi wa Mose pamaso pa Mulungu. Ndipo kunatero kuti m'mawa mwake Mose anakhala pansi kuweruzira anthu milandu yao; ndipo anthu anakhala chilili pamaso pa Mose kuyambira m'mawa kufikira madzulo. Ndipo pamene mpongozi wake wa Mose anaona zonsezi iye anawachitira anthu, anati, Chinthu ichi nchiyani uwachitira anthuchi? Umakhala pa wekha bwanji, ndi anthu onse amakhala chilili pamaso pako kuyambira m'mawa kufikira madzulo? Ndipo Mose anati kwa mpongozi wake, Chifukwa anthu amadza kwa ine kudzafunsira Mulungu; akakhala nao mlandu adza kwa ine, kuti ndiweruze pakati pa munthu ndi mnansi wake, ndi kuti ndiwadziwitse malemba a Mulungu, ndi malamulo ake. Koma mpongozi wa Mose ananena naye, Chinthu uchitachi sichili chabwino ai. Udzalema konse, iwe ndi anthu amene uli nao; pakuti chikukanika chinthu ichi; sungathe kuchichita pa wekha. Tamvera mau anga tsopano, ndikupangire nzeru, ndi Mulungu akhale nawe; ukhale m'malo mwa anthu kwa Mulungu, nupite nayo milandu kwa Mulungu; nuwamasulire malemba, ndi malamulo, ndi kuwadziwitsa njira imene ayenera kuyendamo, ndi ntchito imene ayenera kuchita. Koma iwe, dzisankhire mwa anthu ako onse, amuna amtima, akuopa Mulungu, amuna oona, akudana nalo phindu la chinyengo; nuwaikire iwo oterewa, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, akulu a pa makhumi; ndipo iwo aweruze milandu ya anthu nthawi zonse; ndipo kudzakhala kuti milandu yaikulu yonse abwere nayo kwa iwe; koma milandu yaing'ono yonse aweruze okha; potero idzakuchepera ntchito, ndi iwo adzasenza nawe. Ukachite chinthuchi, ndi Mulungu akakuuza chotero, udzakhoza kupirira, ndi anthu awa onse adzapita kwao mumtendere. Ndipo Mose anamvera mau a mpongozi wake, nachita zonse adazinena. Ndipo Mose anasankha amuna amtima mwa Aisraele onse, nawaika akulu a pa anthu, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, ndi akulu a pa makumi. Ndipo anaweruza anthu nthawi zonse; mlandu wakuwakanika amabwera nao kwa Mose, ndi milandu yaing'ono yonse amaweruza okha. Ndipo Mose analola mpongozi wake amuke; ndipo anachoka kunka ku dziko lake. Mwezi wachitatu atatuluka ana a Israele m'dziko la Ejipito, tsiku lomwelo, analowa m'chipululu cha Sinai. Pakuti anachoka ku Refidimu, nalowa m'chipululu cha Sinai, namanga tsasa m'chipululumo; ndipo Israele anamanga tsasa pamenepo pandunji pa phirilo. Ndipo Mose anakwera kwa Mulungu; ndipo Yehova ali m'phirimo anamuitana, ndi kuti, Uzitero kwa mbumba ya Yakobo, nunene kwa ana a Israele, kuti, Inu munaona chimene ndinachitira Aejipito; ndi kuti ndanyamula inu monga pa mapiko a mphungu, ndi kubwera nanu kwa Ine ndekha. Ndipo tsopano, ngati mudzamvera mau anga ndithu, ndi kusunga chipangano changa, ndidzakuyesani chuma changa cha padera koposa mitundu yonse ya anthu; pakuti dziko lonse lapansi ndi langa; ndipo ndidzakuyesani ufumu wanga wa ansembe, ndi mtundu wopatulika. Awa ndi mau amene ukalankhule ndi ana a Israele. Ndipo Mose anadza, naitana akulu a anthu, nawaikira pamaso pao mau awa onse amene Yehova adamuuza. Ndipo anthu onse anavomera pamodzi, nati, Zonse adazilankhula Yehova tidzazichita. Ndipo Mose anabwera nao mau a anthu kwa Yehova. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndikudza kwa iwe mu mtambo wakuda bii, kuti anthu amve pamene ndilankhula ndi iwe, ndi kuti akuvomereze nthawi zonse. Pakuti Mose adauza Yehova mau a anthuwo. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka kwa anthuwo, nuwapatulitse lero ndi mawa, ndipo atsuke zovala zao. Nakonzekeretu tsiku lachitatu; pakuti tsiku lachitatu Yehova adzatsika pa phiri la Sinai pamaso pa anthu onse. Ndipo ukalembere anthu malire pozungulira, ndi kuti, Muzichenjera musakwere m'phiri, musakhudza chilekezero chake; wokhudza phirilo adzaphedwa ndithu; dzanja lililonse lisalikhudze, wakulikhudza azimponyatu miyala, kapena kumpyoza; ngakhale choweta ngakhale munthu, zisakhale ndi moyo. Pamene lipenga libanika liu lake azikwera m'phirimo. Ndipo Mose anatsika m'phiri kunka kwa anthu, nawapatulitsa anthu; natsuka iwo zovala zao. Ndipo anati kwa anthu, Mukonzekeretu tsiku lachitatu nimusayandikiza mkazi. Ndipo kunali tsiku lachitatu, m'mawa, panali mabingu ndi zimphezi, ndi mtambo wakuda bii paphiripo, ndi liu la lipenga lolimbatu; ndi anthu onse okhala kutsasa ananjenjemera. Ndipo Mose anatulutsa anthu kutsasa, kuti akomane ndi Mulungu; ndipo anaima patsinde pa phiri. Ndipo phiri la Sinai linafuka monsemo, popeza Yehova anatsikira m'moto pamenepo; ndi utsi wake unakwera ngati utsi wa m'ng'anjo, ndi phiri lonse linagwedezeka kwambiri. Ndipo pamene liu la lipenga linamveka linakulirakulira, Mose ananena, ndi Mulungu anamyankha ndi mau. Ndipo Yehova anatsikira pa phiri la Sinai, pamutu pake pa phiri; ndipo Yehova anaitana Mose akwere pamutu pa phiri; ndi Mose anakwerapo. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tsika, chenjeza anthu, kuti angapyolere kwa Yehova kudzaona, ndipo angagwe ambiri a iwowa. Ansembenso, akuyandikiza kwa Yehova adzipatulitse, angawapasule Yehova. Ndipo Mose anati kwa Yehova, Anthu sangathe kukwera m'phiri la Sinai; pakuti Inu mwatichenjeza, ndi kuti, Lemba malire m'phirimo, ndi kulipatula. Ndipo Yehova anati kwa iye, Muka, tsika; nukwere iwe ndi Aroni pamodzi ndi iwe; koma ansembe ndi anthu asapyole kukwera kwa Yehova, angawapasule. Pamenepo Mose anawatsikira anthu, nanena nao. Ndipo Mulungu ananena mau onse amenewa, nati: Ine ndine Yehova Mulungu wako, amene ndinatulutsa iwe ku dziko la Ejipito, kunyumba ya akapolo Usakhale nayo milungu ina koma Ine ndekha. Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m'thambo la kumwamba, kapena za m'dziko lapansi, kapena za m'madzi a pansi pa dziko. Usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje, wakulanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai wa iwo amene akudana ndi Ine; ndi kuwachitira chifundo anthu zikwizikwi a iwo amene akondana ndi Ine, nasunga malamulo anga. Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe; chifukwa Yehova sadzamuyesa iye wosachimwa, amene atchula pachabe dzina lakelo. Udzikumbukira tsiku la Sabata, likhale lopatulika. Masiku asanu ndi limodzi uzigwira, ndi kumaliza ntchito zako zonse; koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata la Yehova Mulungu wako; usagwire ntchito iliyonse, kapena iwe wekha, kapena mwana wako wamwamuna, kapena mwana wako wamkazi, kapena wantchito wako wamwamuna, kapena wantchito wako wamkazi, kapena nyama zako, kapena mlendo amene ali m'mudzi mwako; chifukwa masiku asanu ndi limodzi Yehova adamaliza zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zinthu zonse zili m'menemo, napumula tsiku lachisanu ndi chiwiri; chifukwa chake Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika. Uzilemekeza atate wako ndi amai ako; kuti achuluke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe. Usaphe. Usachite chigololo. Usabe. Usamnamizire mnzako. Usasirire nyumba yake ya mnzako, usasirire mkazi wake wa mnzako, kapena wantchito wake wa mwamuna, kapena wantchito wake wamkazi, kapena ng'ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako. Ndipo anthu onse anaona mabingu ndi zimphezi, ndi liu la lipenga ndi phiri lilikufuka; ndipo pamene anthu anaziona, ananjenjemera, naima patali. Ndipo anati kwa Mose, Mulankhule nafe ndinu, ndipo tidzamva; koma asalankhule nafe Mulungu, kuti tingafe. Ndipo Mose anati kwa anthu, Musaope; pakuti Mulungu wadza kukuyesani ndi kuti kumuopa Iye kukhale pamaso panu, kuti musachimwe Ndipo anthu anaima patali, koma Mose anayandikiza ku mdima waukulu kuli Mulungu. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Uzitero ndi ana a Israele, kuti, Mwapenya nokha kuti ndalankhula nanu, kuchokera kumwamba. Musapange milungu yasiliva ikhale pamodzi ndi Ine; musadzipangire milungu yagolide. Undiumbire guwa la nsembe ladothi, nundiphere pomwepo nsembe zako zopsereza, ndi nsembe zako zamtendere, nkhosa zako ndi ng'ombe zako; paliponse ndikumbukiritsa anthu dzina langa ndidzakudzera ndi kukudalitsa. Ndipo ukandimangira guwa la nsembe lamiyala, usalimanga ndi miyala yosema; ukakwezapo chosemera chako, waliipsa. Kapena usakwere ndi makwerero ku guwa langa la nsembe, kuti angaoneke maliseche ako pamenepo. Ndipo awa ndiwo maweruzo amene uziika pamaso pao. Ukagula mnyamata Muhebri, azigwira ntchito zaka zisanu ndi chimodzi; koma chachisanu ndi chiwiri azituluka waufulu chabe. Akalowa ali yekha azituluka ali yekha; akakhala ndi mkazi, mkazi wake azituluka naye. Akampatsa mkazi mbuye wake, ndipo akambalira ana aamuna ndi aakazi, mkaziyo ndi ana ake azikhala a mbuye wake, ndipo azituluka ali yekha. Koma mnyamatayo akanenetsa, Ndikonda mbuye wanga, mkazi wanga, ndi ana anga; sindituluka waufulu; pamenepo mbuye wake azifika naye kwa oweruza, nafike naye kukhomo, kapena kumphuthu, ndipo mbuye wake amboole khutu lake ndi lisungulo; ndipo iye azimgwirira ntchito masiku onse. Ndipo munthu akagulitsa mwana wake wamkazi akhale mdzakazi, iyeyu asatuluke monga amatuluka anyamata. Akapanda kumkonda mbuye wake, amene anamtoma mwini yekha, azilola kuti amuombole; alibe mphamvu yakumgulitsa kwa anthu achilendo, popeza wachita naye monyenga. Koma ngati amtomera mwana wake wamwamuna, amchitire monga kuyenera ana akazi. Akamtengera mkazi wina, asachepetse chakudya chake, zovala zake, ndi za ukwati zakezake. Ndipo akapanda kumchitira izi zitatu, azituluka chabe, osaperekapo ndalama. Iye amene akantha munthu kotero kuti wafa, aphedwe ndithu. Koma akapanda kumlalira, koma Mulungu akalola akomane ndi mnzake, ndidzakuikirani pothawirapo iye. Koma munthu akachita dala pa mnzake, kumupha monyenga; uzimchotsa ku guwa langa la nsembe, kuti afe. Munthu wakukantha atate wake, kapena amai wake, aphedwe ndithu. Iye wakuba munthu, angakhale wamgulitsa, kapena akampeza m'dzanja lake, aphedwe ndithu. Munthu wakutemberera atate wake, kapena amai wake, aphedwe ndithu. Akalimbana amuna, ndipo wina akakantha mnzake ndi mwala, kapena ndi nkhonya, wosafa iye, koma wakhulungira pakama; akaukanso, nakayendayenda pabwalo ndi ndodo yake, womkanthayo azikhala womasuka; pakutsotsa pake pokha azimbwezera, namchizitse konse. Munthu akakantha mnyamata wake, kapena mdzakazi wake, ndi ndodo, ndipo akafa padzanja pake; ameneyo aliridwe ndithu. Koma akakhala wosafa tsiku limodzi kapena awiri, asalirike, pakuti ndiye ndalama ya mbuye wake. Akayambana amuna, nakakantha mkazi ali ndi pakati, kotero kuti abala, koma alibe kuphwetekwa; alipe ndithu, monga momwe amtchulira mwamuna wa mkaziyo; apereke monga anena oweruza. Koma ngati kuphweteka kukalipo, uzipereka moyo kulipa moyo, diso kulipa diso, dzino kulipa dzino, dzanja kulipa dzanja, phazi kulipa phazi, kutentha kulipa kutentha, bala kulipa bala, mkwapulo kulipa mkwapulo. Munthu akampanda mnyamata wake, kapena mdzakazi wake, padiso, nalithudzula, azimlola amuke waufulu chifukwa cha diso lake. Ndipo akagulula dzino la mnyamata wake, kapena dzino la mdzakazi wake, azimlola amuke waufulu chifukwa cha dzino lake. Ng'ombe ikatunga mwamuna kapena mkazi, nafa, aiponyetu miyala ng'ombeyo, osadya nyama yake; koma mwini ng'ombeyo azimasuka. Koma ngati ng'ombe ikatunga masiku adapitawo, ndipo anamchenjeza mwiniyo, koma osaisunga iye, ndipo ikapha mwamuna kapena mkazi, aiponye miyala ng'ombeyo, ndi mwini wakeyo amuphenso. Akamuikira dipo, azipereka chiombolo cha moyo wake monga mwa zonse adamuikira. Ingakhale yatunga mwana wamwamuna kapena wamkazi, aichitire monga mwa chiweruzo ichi. Ng'ombeyo ikatunga mnyamata kapena mdzakazi, azipatsa mbuye wake ndalama za masekeli a siliva makumi atatu, ndipo ng'ombeyo aiponye miyala. Munthu akafukula dzenje, kapena akakumba dzenje, osalivundikira, ndipo ikagwamo ng'ombe kapena bulu, mwini dzenje azilipa; azilipa ndalama kwa mwini nyamayo, koma yakufayo ndi yake. Ng'ombe ya mwini ikapweteka ng'ombe ya mnzake, nifa, azigulitsa ng'ombe yamoyoyo, nagawe ndalama zake; naigawe, ndi yakufa yomweyo. Kapena kudadziwika kuti ng'ombe ikatunga masiku adapitawo, koma osaisunga mwiniyo, azilipa ndithu, ng'ombe kulipa ng'ombe, koma yakufayo ndi yake. Munthu akaba ng'ombe, kapena nkhosa, nakaipha kapena kuigulitsa, azilipa ng'ombe zisanu pa ng'ombeyo, ndi nkhosa zinai pa nkhosayo. Akampeza wakuba alimkuboola, nakamkantha kotero kuti wafa, palibe chamwazi. Litamtulukira dzuwa, pali chamwazi; wakubayo azilipa ndithu; ngati alibe kanthu, amgulitse pa umbala wake. Akachipeza chakubacho chili m'dzanja lake chamoyo, ngakhale ng'ombe, kapena bulu, kapena nkhosa, alipe mowirikiza. Munthu akadyetsa choweta pabusa kapena pa munda wamphesa, atamasula choweta chake, ndipo chitadya podyetsa pa mwini wake; alipe podyetsa pake poposa, ndi munda wa mphesa wake woposa. Ukayaka moto, nukalandira kuminga, kotero kuti unyeketsa mulu wa tirigu, kapena tirigu wosasenga, kapena munda; woyatsa motoyo alipe ndithu. Munthu akaikiza ndalama kapena chuma kwa mnansi wake, ndipo zibeka m'nyumba ya munthuyo; akapeza mbala, ilipe chowirikiza. Akapanda kumpeza mbalayo, abwere naye mwini nyumbayo kwa oweruza, kumuyesa ngati anaika dzanja lake pa chuma cha mnansi wake. Mlandu uliwonse wa cholakwa, kunena za ng'ombe, za bulu, za nkhosa, za chovala, za kanthu kalikonse kotayika, munthu anenako kali kake; mlandu wa onse awiri ufike kwa oweruza; iye amene oweruza amtsutsa alipe chowirikiza kwa mnansi wake. Munthu akaikiza bulu, kapena ng'ombe, kapena nkhosa, kapena choweta china kwa mnansi wake, ndipo chikafa, kapena chiphwetekwa, kapena wina achipirikitsa osachiona munthu; lumbiro la Yehova likhale pakati pa iwo awiri, kuti sanatulutse dzanja lake pa chuma cha mnansi wake; ndipo mwiniyo azivomereza, ndipo asalipe. Koma ngati chidabedwa kwaoko ndithu, alipe kwa mwiniyo. Ngati chajiwa ndithu, abwere nacho chikhale mboni; asalipe pa chojiwacho. Munthu akabwereka chinthu kwa mnansi wake, ndipo chiphwetekwa, kapena chifa, mwiniyo palibe, azilipa ndithu. Akakhalapo mwiniyo, asalipe; ngati chagwirira ntchito yakulipira, chadzera kulipira kwake. Munthu akanyenga namwali wosapalidwa ubwenzi, nakagona naye, alipetu kuti akhale mkazi wake. Atate wake akakana konse kumpatsa iye, alipe ndalama monga mwa cholipa cha anamwali. Wanyanga usamlola akhale ndi moyo. Aliyense agona ndi choweta aphedwe ndithu. Wakuphera nsembe mulungu wina, wosati Yehova yekha, aonongeke konse. Ndipo usasautsa mlendo kapena kumpsinja; pakuti munali alendo m'dziko la Ejipito. Musazunza mkazi wamasiye, kapena mwana wamasiye aliyense. Ukawazunza ndi kakuti konse, nakandilirira pang'ono ponse iwowa, ndidzamvadi kulira kwao; ndi mkwiyo wanga idzayaka, ndipo ndidzapha inu ndi lupanga; ndipo akazi anu adzakhala amasiye, ndi ana anu omwe. Ukakongoletsa ndalama anthu anga osauka okhala nanu, usamkhalira ngati wangongole; usamwerengera phindu. Ukati ulandire chikole kaya chovala cha mnansi wako, koma polowa dzuwa uchibwezere kwa iye; popeza chofunda chake ndi ichi chokha, ndicho chovala cha pathupi pake; azifundira chiyani pogona? Ndipo kudzakhala kuti akandifuulira Ine, ndidzamva; pakuti Ine ndine wachisomo. Usapeputsa oweruza, kapena kutemberera mkulu wa anthu a mtundu wako. Usachedwa kuperekako zipatso zako zochuluka, ndi zothira zako. Woyamba wa ana ako amuna undipatse Ine. Uzitero nazo ng'ombe zako, ndi nkhosa zako; masiku asanu ndi atatu akhale ndi amai wake; tsiku lachisanu ndi chitatu uzimpereka kwa Ine. Ndipo muzindikhalira Ine anthu opatulika; chifukwa chake musamadya nyama yojiwa kuthengo; itayireni agalu. Usatola mbiri yopanda pake; usathandizana naye woipa ndi kukhala mboni yochititsa chiwawa. Usatsata unyinji wa anthu kuchita choipa; kapena usachita umboni kumlandu, ndi kupatukira kutsata unyinji ndi kukhotetsa mlandu; kapena usakometsera munthu wosauka pa mlandu wake. Ukakomana ndi ng'ombe kapena bulu wa mdani wako zilimkusokera, uzimbwezera izo ndithu. Ukaona bulu wa munthu wakudana nawe alikugona pansi ndi katundu wake, ndipo ukadaleka kuthandiza, koma uzimthandiza ndithu. Usakhotetsa mlandu wa mnzako waumphawi. Uzikhala kutali ndi mlandu wonama; ndipo usapha munthu wosachimwa ndi wolungama; pakuti sindidzayesa wolungama munthu woipa. Usalandira chokometsera mlandu; pakuti chokometsera mlandu chidetsa maso a openya, nichisanduliza mlandu wa olungama. Usampsinja mlendo; pakuti mudziwa mtima wa mlendo popeza munali alendo m'dziko la Ejipito. Ndipo uzibzala m'munda mwako zaka zisanu ndi chimodzi, ndi kututa zipatso zako; koma chaka chachisanu ndi chiwiri uuleke, ugone; kuti aumphawi a anthu a mtundu wako adyemo, ndipo zotsalira nyama za kuthengo zizidye; momwemo uzichita ndi munda wako wamphesa, ndi munda wako wa azitona. Uzichita ntchito yako masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri uzipumula; kuti ng'ombe yako ndi bulu wako zipumule, ndi kuti mwana wa mdzakazi wako ndi mlendo atsitsimuke. Ndipo samalirani zonse ndanena ndi inu; nimusatchule dzina la milungu ina; lisamveke pakamwa pako. Muzindichitira Ine madyerero katatu m'chaka. Uzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa; masiku asanu ndi awiri uzidya mkate wopanda chotupitsa, monga ndinakuuza, nyengo yoikika, mwezi wa Abibu, pakuti m'menemo unatuluka m'Ejipito; koma asaoneke munthu pamaso panga opanda kanthu; ndi chikondwerero cha Masika, zipatso zoyamba za ntchito zako, zimene udazibzala m'munda; ndi chikondwerero cha Kututa, pakutha chaka, pamene ututa ntchito zako za m'munda. Katatu m'chaka amuna onse azioneka pamaso pa Ambuye Yehova. Usapereka mwazi wa nsembe yanga pamodzi ndi mkate wachotupitsa; ndi mafuta a madyerero anga asagonamo kufikira m'mawa. Uzibwera nazo zoyambayamba za m'munda mwako kunyumba ya Yehova Mulungu wako. Usaphike mwanawambuzi mu mkaka wa make. Taona, ndituma mthenga akutsogolere, kukusunga panjira, ndi kukufikitsa pamaso pomwe ndakonzeratu. Musamalire iye, ndi kumvera mau ake; musamwawitsa mtima, pakuti sadzakhululukira zolakwa zanu; popeza dzina langa lili m'mtima mwake. Pakuti ukamveratu mau ake, ndi kuchita zonse ndizilankhula, ndidzakhala mdani wa adani ako, ndipo ndidzasautsa akusautsa iwe. Pakuti mthenga wanga adzakutsogolera, nadzakufikitsa kwa Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, ndi Akanani, Ahivi, ndi Ayebusi; ndipo ndidzawaononga. Usagwadira milungu yao, kapena kuwatumikira, kapena kuchita monga mwa ntchito zao; koma uwapasule konse, ndi kugamulatu zoimiritsa zao. Ndipo muzitumikira Yehova Mulungu wanu, potero adzadalitsa chakudya chako, ndi madzi ako; ndipo ndidzachotsa nthenda pakati pa iwe. M'dziko mwanu simudzakhala wakutaya mwana, kapena wosabala; ndidzakwaniritsa kuwerenga kwa masiku ako. Ndidzatumiza kuopsa kwanga kukutsogolere, ndipo ndidzapirikitsa anthu onse amene udzafika kwao, ndipo ndidzachita kuti adani ako onse adzakuonetsa m'mbuyo mwao. Ndipo ndidzatumiza mavu akutsogolere amene adzaingitsa Ahivi, Akanani, ndi Ahiti, pamaso pako. Sindidzawaingitsa pamaso pako chaka chimodzi; kuti dziko lingakhale bwinja, ndi zilombo za kuthengo zingakuchulukire. Ndidzawaingitsa pang'onopang'ono pamaso pako, kufikira utachuluka, ndi kulandira dziko cholowa chako. Ndipo ndidzalemba malire ako kuyambira ku Nyanja Yofiira, kufikira ku nyanja ya Afilisti, ndi kuyambira kuchipululu kufikira ku Nyanja; popeza ndidzapereka okhala m'dzikolo m'dzanja lako, ndipo uziwaingitsa pamaso pako. Usapangana nao, kapena ndi milungu yao. Asakhale m'dziko lako iwowa, kuti angakulakwitse pa Ine; pakuti ukatumikira milungu yao, kudzakukhalira msampha ndithu. Ndipo Iye ananena ndi Mose, Ukwere kudza kwa Yehova, iwe ndi Aroni, Nadabu ndi Abihu, ndi akulu a Israele makumi asanu ndi awiri; ndipo mugwadire pakudza kutali; ndipo Mose yekha ayandikire kwa Yehova; koma asayandikire iwowa; ndi anthunso asakwere naye. Ndipo Mose anadza nafotokozera anthu mau onse a Yehova, ndi maweruzo onse; ndipo anthu onse anavomera pamodzi, nati, Mau onse walankhula Yehova tidzachita. Ndipo Mose analembera mau onse a Yehova, nalawira kuuka mamawa, namanga guwa la nsembe patsinde pa phiri, ndi zoimiritsa khumi ndi ziwiri, kwa mafuko khumi ndi awiri a Israele. Ndipo anatuma ana a Israele a misinkhu ya anyamata, ndiwo anapereka nsembe zopsereza, naphera Yehova nsembe zamtendere, za ng'ombe. Ndipo Mose anagawa mwaziwo, nathira wina m'zotengera, nawaza wina pa guwa la nsembe Ndipo anatenga buku la Chipangano, nawerenga m'makutu a anthu; ndipo iwo anati, Zonse zimene Yehova walankhula tidzachita, ndi kumvera. Ndipo Mose anatenga mwaziwo, nawaza pa anthu, nati Taonani mwazi wa chipangano, chimene Yehova anachita nanu, kunena za mau awa onse. Ndipo Mose ndi Aroni, Nadabu ndi Abihu, ndi akulu a Israele makumi asanu ndi awiri anakwerako; ndipo anapenya Mulungu wa Israele; ndipo pansi pa mapazi ake panali ngati mayalidwe oyera a miyala yasafiri, ndi ngati thupi la thambo loti mbee. Koma sanatulutse dzanja lake pa akulu a ena a Israele; ndipo anapenya Mulungu, nadya, namwa. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ukwere kudza kwa Ine m'phiri muno, nukhale pompano; ndipo ndidzakupatsa magome amiyala, ndi chilamulo ndi malamulo ndawalembera kuti uwalangize. Ndipo anauka Mose, ndi Yoswa mtumiki wake; ndipo Mose anakwera m'phiri la Mulungu. Ndipo anati kwa akulu, Tilindeni kuno kufikira tidzabwera kwa inu; ndipo taonani, Aroni ndi Huri ali nanu; munthu akakhala ndi mlandu abwere kwa iwowa. Ndipo Mose anakwera m'phirimo, ndi mtambo unaphimba phirilo. Ndipo ulemerero wa Yehova unakhalabe pa phiri la Sinai, ndi mtambo unaliphimba masiku asanu ndi limodzi; ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri Iye ali m'kati mwa mtambo anaitana Mose. Ndipo maonekedwe a ulemerero wa Yehova anali ngati moto wonyeketsa pamwamba pa phiri, pamaso pa ana a Israele. Ndipo Mose analowa m'kati mwa mtambo, nakwera m'phirimo; ndipo Mose anakhala m'phiri masiku makumi anai usana ndi usiku. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Lankhula ndi ana a Israele, kuti anditengere chopereka; ulandire chopereka changa kwa munthu aliyense mtima wake umfunitsa mwini. Ndipo choperekacho uchilandire kwa iwo ndi ichi: golide, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ubweya wa mbuzi; ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, ndi mtengo wakasiya; mafuta akuunikira, zonunkhira za mafuta odzoza, ndi za chofukiza cha fungo lokoma; miyala yaberulo, ndi miyala yoika paefodi, ndi pachapachifuwa. Ndipo andimangire malo opatulika; kuti ndikhale pakati pao. Monga mwa zonse Ine ndilikuonetsa iwe, chifaniziro cha Kachisi, ndi chifaniziro cha zipangizo zake zonse, momwemo uchimange. Ndipo azipanga likasa la mtengo wakasiya: utali wake mikono iwiri ndi hafu, kupingasa kwake mkono ndi hafu, msinkhu wake mkono ndi hafu. Ndipo ulikute ndi golide woona, ulikute m'kati ndi kubwalo, nulipangire mkombero wagolide pozungulira pake. Ndipo uliyengere mphete zinai zagolide, ndi kuziika kumiyendo yake inai; mphete ziwiri pa mbali yake ina, ndi mphete ziwiri pa ina. Ndipo uzipanga mphiko za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi golide. Nupise mphiko m'mphetezo pa mbali zake za likasa, zakunyamulira nazo likasalo. Mphiko zikhale m'zimphete za likasa; asazisolole. Ndipo uziika m'likasamo mboni imene ndidzakupatsa. Ndipo uzipanga chotetezerapo cha golide woona; utali wake mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwake mkono ndi hafu. Uzipanganso akerubi awiri agolide; uwasule mapangidwe ake, pa mathungo ake awiri a chotetezerapo. Nupange kerubi mmodzi ku thungo lino, ndi kerubi wina ku thungo lina; upange akerubi ochokera kuchotetezerapo, pa mathungo ake awiri. Ndipo akerubi afunyululire mapiko ao m'mwamba, ndi kuphimba chotetezerapo ndi mapiko ao, ndi nkhope zao zipenyane; nkhope za akerubi zipenye kuchotetezerapo. Ndipo uziika chotetezerapo pamwamba pa likasa, ndi kuikamo mboni ndidzakupatsayo m'likasamo. Ndipo pomwepo ndidzakomana ndi iwe, ndi kulankhula ndi iwe, ndili pamwamba pa chotetezerapo, pakati pa akerubi awiriwo okhala pa likasa la mboni, zonse zimene ndidzakuuza za ana a Israele. Ndipo uzipanga gome la mtengo wakasiya; utali wake mikono iwiri, ndi kupingasa kwake mkono umodzi, ndi msinkhu wake mkono ndi hafu. Ndipo ulikute ndi golide woona ndi kulipangira mkombero wagolide pozungulira pake. Nulipangire mitanda pozungulirapo yoyesa chikhato m'kupingasa kwake, ndi pamitanda pake pozungulira upangirepo mkombero wagolide. Nulipangire mphete zinai zagolide, ndi kuika mphetezo pangodya zinai zokhala pa miyendo yake inai. Mphetezo zikhale pafupi pa mitanda, zikhale zopisamo mphiko za kunyamulira nazo gome. Ndipo uzipanga mphiko za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi golide, kuti anyamulire nazo gome. Ndipo uzipanga mbale zake, ndi zipande zake, ndi mitsuko yake, ndi zikho zake zakuthira nazo; uzipanga za golide woona. Ndipo uziika mkate woonekera pa gomelo pamaso panga nthawi zonse. Ndipo uzipanga choikapo nyali cha golide woona; choikapocho chisulidwe mapangidwe ake, tsinde lake ndi thupi lake; zikho zake, mitu yake, ndi maluwa ake zikhale zochokera m'mwemo; ndipo m'mbali zake mutuluke mphanda zisanu ndi imodzi; mphanda zitatu za choikapo nyalicho zituluke m'mbali yake ina, ndi mphanda zitatu za choikapo nyalicho zituluke m'mbali inzake. Ku mphanda ina kukhale zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi luwa; ndi ku mphanda inzake zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi luwa; zitere mphanda zisanu ndi imodzi zotuluka m'choikapo nyalicho. Ndipo pa choikapo nyali chomwe pakhale zikho zinai zopangika ngati katungurume, mitu yake ndi maluwa ake; pakhale mutu pansi pa mphanda ziwiri zotuluka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri zotuluka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri zotuluka m'mwemo; itere ku mphanda zisanu ndi imodzi zotuluka m'choikapo nyalicho. Mitu yao ndi mphanda zao zikhale zotuluka m'mwemo; chonsechi chikhale chosulika chimodzi cha golide woona. Ndipo uzipanga nyali zake, zisanu ndi ziwiri; ndipo ayatse nyali zake, ziwale pandunji pake. Ndipo mbano zake, ndi zoolera zake, zikhale za golide woona. Achipange ichi ndi zipangizo izi zonse za talente wa golide woona. Ndipo uyang'anire uzipanga monga mwachifaniziro chao, chimene anakuonetsa m'phirimo. Ndipo uzipanga Kachisi ndi nsalu zophimba khumi, za bafuta wa thonje losansitsa, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira; uombemo akerubi, ntchito ya mmisiri. Utali wake wa nsalu yophimba imodzi ndiwo mikono makumi awiri kudza isanu ndi itatu, ndi kupingasa kwa nsalu imodzi ndiko mikono inai; nsalu zonse zikhale za muyeso umodzi. Nsalu zisanu zilumikizane ina ndi inzake; ndi nsalu zisanu zina zilumikizane ina ndi inzake. Ndipo uziika magango a nsalu ya madzi m'mphepete mwake mwa nsalu imodzi, ku mkawo wa chilumikizano; nuchite momwemo m'mphepete mwake mwa nsalu ya kuthungo ya chilumikizano china. Uziika magango makumi asanu pa nsalu yochingira imodzi, nuikenso magango makumi asanu m'mphepete mwake mwa nsalu ya chilumikizano china; ndipo magango akomanizane lina ndi linzake. Uzipanganso zokowera makumi asanu zagolide, ndi kumanga nsaluzo pamodzi ndi zokowerazo; kuti Kachisi akhale mmodzi. Ndipo uziomba nsalu zophimba za ubweya wa mbuzi zikhale hema pamwamba pa Kachisi; uziomba nsalu khumi ndi imodzi. Utali wake wa nsalu imodzi ndiwo mikono makumi atatu, ndi kupingasa kwake kwa nsalu imodzi ndiko mikono inai; nsalu khumi ndi imodzi zikhale za muyeso womwewo. Nuzisoka pamodzi nsalu zisanu pa zokha, ndi nsalu zisanu ndi imodzi pa zokha, nupinde nsalu yachisanu ndi chimodziyo pa khomo la hema. Ndipo uziika magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu imodzi, ya kuthungo ya chilumikizano, ndi magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu ya kuthungo ya chilumikizano china. Ndipo uzipanga zokowera makumi asanu zamkuwa, ndi kukowetsa zokowerazo m'magangomo, ndi kumanga pamodzi hemalo likhale limodzi. Ndipo chotsalacho pa nsalu za hemalo, hafu yake ya nsalu yotsalirayo, ichinge pambuyo pake pa Kachisi. Ndi mkono wa pa mbali yino, ndi mkono wa pa mbali inzake, wakutsalira m'utali wake wa nsalu za hemalo, ichinge pambali zake za Kachisi, mbali yino ndi mbali ina, kumphimba. Ndipo uzipangira hema chophimba cha zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi chophimba za zikopa za akatumbu pamwamba pake. Ndipo uzipangira Kachisi matabwa oimirika, a mtengo wakasiya. Utali wake wa thabwa limodzi ndiwo mikono khumi, ndi kupingasa kwake kwa thabwali mkono ndi hafu. Pa thabwa limodzi pakhale mitsukwa iwiri, yomangika pamodzi; uzitero pa matabwa onse a Kachisi. Ndipo uzipanga matabwa a Kachisi, matabwa makumi awiri ku mbali ya kumwera, kumwera. Nuzipanga makamwa makumi anai asiliva pansi pa matabwa makumi awiri; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi kwa mitsukwa yake iwiri, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina kwa mitsukwa yake iwiri; ndi pa mbali yake ina ya Kachisi, mbali ya kumpoto, pakhale matabwa makumi awiri; ndi makamwa asiliva makumi anai; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina. Ndipo uzipanga matabwa asanu ndi limodzi kwa mbali ya Kachisi ya kumbuyo. Nupange matabwa awiri angodya za Kachisi za kumbuyo. Ndipo akhale ophatikizika pamodzi patsinde, nakhalenso ophatikizika pamodzi kumutu kwake ndi mphete imodzi; azitero onse awiri; azikhala angodya ziwiri. Ndipo pakhale matabwa asanu ndi atatu, ndi makamwa ao asiliva, ndiwo makamwa khumi mphambu asanu ndi limodzi; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina. Ndipo uzipanga mitanda ya mtengo wakasiya; isanu ya matabwa a pa mbali ina ya Kachisi, ndi mitanda isanu ya matabwa a pa mbali ina ya Kachisi, ndi mitanda isanu ya matabwa a pa mbali ya Kachisi ya kumbuyo kumadzulo. Ndi mtanda wa pakati pa matabwa ufikire kuthungo. Ndipo uzikuta matabwa ndi golide, ndi kupanga mphete zao zagolide zopisamo mitandayo; uzikutanso mitandayo ndi golide. Ndipo uutse Kachisi monga mwa makhalidwe ake amene anakusonyeza m'phiri. Ndipo uziomba nsalu yotchinga ya thonje lamadzi, ndi lofiirira ndi lofiira, ndi la bafuta wa thonje losansitsa, aiombe ndi akerubi ntchito ya mmisiri; ndipo uichinge pa mizati inai ya mitengo wakasiya, zokuta ndi golide; zokowera zao zikhale zagolide, ndi makamwa anai asiliva. Ndipo uzitchinga nsalu yotchinga pa zokowerazo, nulowetse likasa la mboni kukati kwa nsalu yotchinga; ndipo nsalu yotchingayo idzakugawirani pakati pa malo opatulika ndi malo opatulika kwambiri. Ndipo uziika chotetezerapo pa likasa la mboni, m'malo opatulika kwambiri. Nuziika gomelo kunja kwa nsalu yotchinga, ndi choikapo nyali pandunji pa gome, pa mbali ya kumwera ya Kachisi; koma uike gomelo pa mbali ya kumpoto. Ndipo uziomba nsalu yotsekera pa khomo la hema, ya lakuda, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya wopikula. Ndipo uzipangira nsalu yotsekerayo nsanamira zisanu za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi golide; zokowera zao zikhale zagolide; nuziyengera makamwa asanu amkuwa. Ndipo upange guwa la nsembe la mtengo wakasiya, utali wake mikono isanu, ndi kupingasa kwake mikono isanu, guwa la nsembelo likhale laphwamphwa, ndi msinkhu wake mikono itatu. Ndipo uzipanga nyanga zake pangodya zake zinai; nyanga zake zikhale zotuluka m'mwemo: nulikute ndi mkuwa. Ndipo uzipanga zotayira zake zakulandira mapulusa ake, ndi zoolera zake, ndi mbale zowazira zake, ndi mitungo yake, ndi zopalira moto zake; zipangizo zake zonse uzipanga zamkuwa. Ndipo ulipangire sefa, malukidwe ake ndi amkuwa; nupange pa malukidwewo ngodya zake zinai mphete zinai zamkuwa. Nuwaike pansi pa khoma lamkati la guwa la nsembelo posungulira, kuti malukidwe alekeze pakati pa guwa la nsembelo. Ndipo upangire guwa la nsembe mphiko, mphiko za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi mkuwa. Ndipo apise mphiko m'mphetezo kuti mphikozo zikhale pa mbali ziwiri za guwa la nsembe polinyamula. Ulipange lagweregwere ndi matabwa; monga anakuonetsa m'phirimo; alipange momwemo. Upangenso bwalo la chihema; pa mbali yake ya kumwera, kumwera, pakhale nsalu zochingira za kubwalo za nsalu yabafuta wa thonje losansitsa, utali wake wa pa mbali imodzi mikono zana; ndi nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ao makumi awiri akhale amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zikhale zasiliva. Momwemonso pa mbali ya ku kumpoto m'utali mwake pakhale nsalu zochingira za mikono zana limodzi m'utali mwake; ndi nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ao akhale amkuwa; zokowera za nsichizo ndi mitanda yake zikhale zasiliva. Ndipo m'kupingasa kwa bwaloli pa mbali ya kumadzulo mukhale nsalu zochingira za mikono makumi asanu; nsichi zake zikhale khumi, ndi makamwa ao khumi. Ndipo m'kupingasa kwake kwa bwalo pa mbali ya kum'mawa, kum'mawa, mukhale mikono makumi asanu. Ndi nsalu zochingira za pa mbali imodzi ya kuchipata zikhale za mikono khumi ndi isanu; nsichi zake zikhale zitatu, ndi makamwa ao atatu. Ndi pa mbali ina pakhale nsalu zochingira za mikono khumi ndi isanu; nsichi zake zikhale zitatu, ndi makamwa ao atatu. Ndipo pa chipata cha bwalolo pakhale nsalu yotsekera ya mikono makumi awiri, ya lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya wopikula; nsichi zake zikhale zinai, ndi makamwa ao anai. Nsichi zonse za pabwalo pozungulira zimangike pamodzi ndi mitanda yasiliva; zokowera zao zasiliva, ndi makamwa ao amkuwa. Utali wake wa bwalolo ukhale wa mikono zana limodzi, ndi kupingasa kwake makumi asanu monsemo, ndi msinkhu wake wa mpanda mikono isanu; ukhale wabafuta wa thonje losansitsa; ndi makamwa a nsichizo akhale amkuwa. Zipangizo zonse za Kachisi, m'machitidwe ake onse, ndi zichiri zake zonse, ndi zichiri zonse za bwalo lake, zikhale zamkuwa. Ndipo uuze ana a Israele akutengere mafuta a azitona oyera opera akuunikira, kuti awalitse nyali kosalekeza. Aroni ndi ana ake aikonze m'chihema chokomanako, kunja kwa nsalu yotchinga yokhala kumboni, kuyambira madzulo kufikira m'mawa; likhale lemba losatha mwa mibadwo yao, alisunge ana a Israele. Ndipo akuyandikire Aroni mbale wako, ndi ana ake amuna pamodzi naye, mwa ana a Israele, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe, ndiwo Aroni, Nadabu, ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni. Ndipo usokere Aroni mbale wako zovala zopatulika, zikhale zaulemerero ndi zokoma. Ndipo ulankhule ndi onse a mtima waluso, amene ndawadzaza ndi mzimu waluso, kuti amsokere Aroni zovala apatulidwe nazo, andichitire Ine ntchito ya nsembe. Ndipo zovala azisoka ndizi: chapachifuwa ndi efodi, ndi mwinjiro, ndi malaya opikapika, ndi nduwira, ndi mpango; tero apangire Aroni mbale wako ndi ana ake zovala zopatulika, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe. Ndipo atenge golide, ndi lamadzi ndi lofiirira ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa. Naombe efodi ndi golide, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya mmisiri. Akhale nazo zapamapewa ziwiri zomangika ku nsonga zake ziwiri, kuti amangike nazo. Ndipo mpango wa efodi, wokhala pamenepo, kuti ammange nao, ukhale wa chiombedwe chomwecho, ndi woombera kumodzi, wagolide, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa. Ndipo utenge miyala iwiri yaberulo, nulochepo maina a ana a Israele; maina asanu ndi limodzi pa mwala wina, ndi maina asanu ndi limodzi otsala pa mwala unzake, mwa kubadwa kwao. Uloche miyala iwiriyo ndi maina a ana a Israele, monga mwa ntchito ya wolocha miyala, monga malembedwe a chosindikizira, uipange igwirike ndi zoikamo zagolide. Ndipo uiike miyala iwiriyo pa zapamapewa za efodi, ikhale miyala ya chikumbutso cha ana a Israele; ndipo Aroni azinyamula maina ao pa mapewa ake awiri, akhale chikumbutso pamaso pa Yehova. Ndipo upange zoikamo za golide; ndi maunyolo awiri a golide woona; uwapote ngati zingwe, ntchito yopota; numange maunyolo opotawo pazoikamo. Upangenso chapachifuwa cha chiweruzo, ntchito ya mmisiri; uchiombe mwa chiombedwe cha efodi; uchiombe ndi golide, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa. Chikhale chaphwamphwa, chopindika, utali wake dzanja limodzi, ndi kupingasa kwake dzanja limodzi. Ndipo uikepo miyala yoikikapo, mizere inai ya miyala; mzere wa odemu, pitida, ndi bareketi, ndiyo ya mzere woyamba; ndi mzere wachiwiri wa nofeki, safiro, ndi yahaloni; ndi mizere wachitatu wa lesemu, sibu, ndi akalama; ndi mzere wachinai wa tarisisi, sohamu, ndi yasefe; zikhale zogwirika ndi golide m'zoikamo zao. Ndi miyalayi ikhale monga mwa maina a ana a Israele, khumi ndi awiri, monga maina ao; monga malochedwe a chosindikizira, yonse ikhale monga maina ao, kwa mafuko khumi ndi awiri. Upangenso maunyolo pa chapachifuwa ngati zingwe, ntchito yopota, ya golide woona. Nupangire pa chapachifuwa mphete ziwiri zagolide, ndi kuzika mphete ziwirizo pa nsonga zake ziwiri za chapachifuwa. Numange maunyolo awiri opota agolide ku mphete ziwirizo pa nsonga pake pa chapachifuwa. Koma nsonga zake ziwiri za maunyolo opotawo uzimange ku zoikamo ziwiri, ndi kuziika pa zapamapewa ziwiri za efodi, m'tsogolo mwake. Ndipo upange mphete ziwiri zagolide, ndi kuzimanga pa nsonga zake ziwiri za chapachifuwa, m'mphepete mwake, m'katimo ku mbali ya kuefodi. Upangenso mphete ziwiri zagolide, ndi kuzimanga pa zapamapewa ziwiri za efodi, m'munsi, ku mbali yake ya kutsogolo, pafupi pa msoko wake, pamwamba pa mpango wa efodi. Ndipo amange chapachifuwa pa mphete zake ndi mphete za efodi ndi mkuzi wamadzi, kuti chikhale pa mpango wa efodi; ndi kuti chapachifuwa chisamasuke paefodi. Ndipo Aroni azinyamula maina a ana a Israele pa chapachifuwa cha chiweruzo pamtima pake, pakulowa iye m'malo opatulika, akhale chikumbutso pankhope pa Yehova kosalekeza. Ndipo uike Urimu ndi Tumimu mwa chapachifuwa cha chiweruzo; ndipo zikhale pa mtima wa Aroni, pakulowa iye pamaso pa Yehova; ndipo Aroni azinyamula chiweruzo cha ana a Israele pamtima pake pamaso pa Yehova kosalekeza. Ndipo uombe mwinjiro wa efodi ndi lamadzi lokha. Ndipo polowa mutu pakhale pakati pake; pakhale mkawo pozungulira polowa pake, wa ntchito yoomba, ngati polowa pa malaya otchinjiriza, pangang'ambike. Ndipo pa mbinyiru wake upange makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, pambinyiru pake pozungulira, ndi kuwapakiza ndi miliu yagolide pozungulira; mliu wa golide ndi khangaza, mliu wagolide ndi khangaza, pa mbinyiru wa mwinjiro pozungulira. Ndipo Aroni auvale kuti atumikire nao; ndipo limveke liu lake pakulowa iye m'malo opatulika pamaso pa Yehova, ndi pakutuluka iye, kuti asafe. Ndipo upange golide waphanthiphanthi woona, ndi kulochapo, monga malochedwe a chosindikizira, Kupatulikira Yehova. Nuchiike pamkuzi wamadzi, ndipo chikhale panduwira, chikhale patsogolo pake pa nduwira. Ndipo chizikhala pamphumi pake pa Aroni, ndipo Aroni azinyamula mphulupulu ya zopatulidwa, zimene ana a Israele azipatulira, ndi zopereka zao zonse zopatulira; ndipo chizikhala pamphumi pake kosalekeza, kuti alandiridwe pamaso pa Yehova. Ndipo upikule malaya am'kati abafuta a thonje losansitsa, nusoke nduwira wabafuta, nusokenso mpango wopikapika. Ndipo usokere ana a Aroni malaya am'kati, nuwasokere mipango; uwasokerenso akapa akhale aulemerero ndi okoma. Ndipo uveke nazo Aroni mbale wako, ndi ana ake omwe; ndi kuwadzoza, ndi kudzaza dzanja lao, ndi kuwapatula, andichitire Ine ntchito ya nsembe. Uwasokerenso zovala za miyendo za bafuta wa thonje losansitsa kubisa maliseche ao; ziyambire m'chuuno zifikire kuntchafu. Ndipo azivale Aroni ndi ana ake, pakulowa iwo ku chihema chokomanako, kapena poyandikiza iwo kuguwa la nsembe kutumikira m'malo opatulika; anganyamule mphulupulu, nangafe; likhale lemba losatha la iye ndi mbumba zake pambuyo pake. Ichi ndicho uwachitire kuwapatula, andichitire ntchito ya nsembe: tenga ng'ombe yamphongo, ndi nkhosa ziwiri zamphongo zangwiro, ndi mkate wopanda chotupitsa, ndi timitanda topanda chotupitsa tosanganiza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda chotupitsa, todzoza ndi mafuta; utipange ndi ufa wosalala watirigu. Ndipo uziike mu dengu limodzi, ndi kubwera nazo mudengu, pamodzi ndi ng'ombe yamphongo ndi nkhosa ziwiri zamphongo. Ndipo ubwere nao Aroni ndi ana ake amuna ku khomo la chihema chokomanako, ndi kuwasambitsa m'madzi. Pamenepo utenge zovalazo ndi kuveka Aroni malaya am'kati, ndi mwinjiro wa efodi, ndi efodi, ndi chapachifuwa, ndi kummangira m'chuuno ndi mpango wa efodi woluka mwanzeru; ndipo uike nduwira pamutu pake, ndi kuika korona wopatulika panduwirapo. Pamenepo utenge mafuta odzoza nao nuwatsanulire pamutu pake, ndi kumdzoza. Ndipo ubwere nao ana ake amuna ndi kuwaveka malaya am'kati. Uwamangirenso Aroni ndi ana ake amuna mipango m'chuuno mwao, nuwamangire akapa pamutu pao; ndipo akhale ansembe mwa lemba losatha; nudzaze dzanja la Aroni ndi dzanja la ana ake amuna. Ndipo ubwere nayo ng'ombe yamphongo patsogolo pa chihema chokomanako; ndipo Aroni ndi ana ake amuna aike manja ao pamutu pa ng'ombe yamphongoyo. Nuphe ng'ombe yamphongoyo pamaso pa Yehova, pa khomo la chihema chokomanako. Pamenepo utapeko pa mwazi wa ng'ombe yamphongo, ndi kuupaka pa nyanga za guwa la nsembe ndi chala chako, nutsanulire mwazi wonse pa tsinde la guwa la nsembe. Nutenge mafuta onse akukuta matumbo, ndi chokuta cha mphafa ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pa izo, ndi kuzitentha pa guwa la nsembe. Koma nyama ya ng'ombeyo, ndi chikopa chake, ndi chipwidza chake, uzitentha izi ndi moto kunja kwa chigono; ndiyo nsembe yauchimo. Utengenso nkhosa yamphongo imodziyo; ndi Aroni ndi ana ake amuna aike manja ao pamutu pa nkhosa yamphongoyo. Nuiphe nkhosa yamphongoyo, ndi kutenga mwazi wake, ndi kuuwaza pa guwa la nsembe pozungulira. Ndipo upadzule nkhosa yamphongo m'ziwalo zake, ndi kutsuka matumbo ake, ndi miyendo yake, ndi kuziika pa ziwalo zake, ndi pamutu pake. Pamenepo upsereze nkhosa yamphongo yonse pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza ya Yehova, ya fungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya Yehova. Ndipo utenge nkhosa yamphongo yinayo; ndi Aroni ndi ana ake amuna aike manja ao pamutu pa nkhosa yamphongoyo. Pamenepo uiphe nkhosa yamphongoyo, nutapeko pa mwazi wake, ndi kuupaka pa ndewerere ya khutu lamanja la Aroni, ndi pa ndewerere ya khutu lamanja ana ake amuna, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lao lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lao lamanja ndi kuuwaza mwaziwo pa guwa la nsembe posungulira. Ndipo utapeko pamwazi uli pa guwa la nsembe, ndi pa mafuta akudzoza nao, ndi kuwaza pa Aroni, ndi pa zovala zake, ndi pa ana ake amuna, ndi pa zovala za ana ake amuna, pamodzi ndi iye; kuti akhale wopatulidwa, ndi zovala zake zomwe, ndi ana ake amuna ndi zovala zao zomwe pamodzi ndi iye. Utengenso mafuta a nkhosa yamphongoyo, ndi mchira, chokuta cha mphafa, ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pamenepo, ndi mwendo wam'mwamba wa ku dzanja lamanja; pakuti ndiyo nkhosa yamphongo ya kudzaza manja; ndi mkate wamphumphu umodzi, ndi kamtanda ka mkate wosanganiza ndi mafuta, ndi kamtanda kamodzi kaphanthi, zili mu dengu la mkate wopanda chotupitsa wokhala pamaso pa Yehova; ndipo uike zonsezi m'manja a Aroni, ndi m'manja a ana ake amuna; nuziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova. Pamenepo uzilandire m'manja mwao, ndi kuzipsereza pa guwa la nsembe, pa nsembe yopsereza, zichite fungo lokoma pamaso pa Yehova; ndiyo nsembe yamoto ya Yehova. Ndipo utenge nganga ya nkhosa yamphongo yodzaza manja ya Aroni, ndi kuiweyula ikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndipo ikhale gawo lako. Ndipo upatule nganga ya nsembe yoweyula, ndi mwendo wam'mwamba wa nsembe yokweza, imene anaiweyula, ndi imene anaikweza, za nkhosa yamphongo yakudzaza manja; zili za Aroni, ndi za ana ake amuna; ndipo zikhale za Aroni ndi za ana ake amuna, mwa lemba losatha, ziwadzere kwa ana a Israele; popeza ndiyo nsembe yokweza; ndipo ikhale nsembe yokweza yodzera kwa ana a Israele, ya kwa nsembe zamtendere zao, ndiyo nsembe yao yokweza ya Yehova. Ndipo zovala zopatulika za Aroni zikhale za ana ake amuna pambuyo pake, kuti awadzoze atazivala, nadzaze manja ao atazivala; mwana wake wamwamuna amene adzakhala wansembe m'malo mwake azivala masiku asanu ndi awiri, pakulowa iye m'chihema chokomanako kutumikira m'malo opatulika. Ndipo utenge nkhosa yamphongo yodzaza manja, nuphike nyama yake m'malo opatulika. Ndipo Aroni ndi ana ake amuna adye nyama ya nkhosa yamphongoyo, ndi mkate uli mudengu, pa khomo la chihema chokomanako. Ndipo adye zimene anachita nazo choteteza, kuti awadzaze manja ndi kuwapatulitsa; koma mlendo asadyeko, pakuti nzopatulika izi. Ndipo ikatsalako nyama yodzaza manja, kapena mkate kufikira m'mawa, pamenepo utenthe zotsalazo ndi moto; asazidye popeza nchopatulika ichi. Ndipo utero nao Aroni, ndi ana ake amuna, monga mwa zonse ndakuuza; udzaze manja ao masiku asanu ndi awiri. Nukonze ng'ombe yamphongo, ndiyo nsembe yauchimo yakuteteza nayo, tsiku ndi tsiku; ndipo uyeretsa guwa la nsembe, pakuchita choteteza pamenepo; ndipo ulidzoze kulipatula. Uchitire guwa la nsembe choteteza masiku asanu ndi awiri ndi kulipatula; ndipo guwa la nsembelo likhale lopatulika kwambiri; chilichonse chikhudza guwa la nsembelo chikhale chopatulika. Koma izi ndizo uzikonza pa guwa la nsembelo; anaankhosa awiri a chaka chimodzi, tsiku ndi tsiku kosalekeza. Mwanawankhosa wina ukonze m'mawa; ndi mwanawankhosa wina ukonze madzulo; ndi pa mwanawankhosa mmodziyo pakhale limodzi la magawo khumi la ufa wosalala, wosanganiza ndi limodzi la magawo anai la hini wa mafuta opera; ndi limodzi la magawo anai la hini wa vinyo, likhale nsembe yothira. Ndi mwanawankhosa wina ukonze madzulo; umkonze umo unachitira nsembe yaufa cha m'mawa ndi nsembe yake yothira, akhale fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova. Ikhale nsembe yopsereza yosalekeza ya mwa mibadwo yanu, pa khomo la chihema chokomanako, pamaso pa Yehova, kumene ndidzakomana nanu, kulankhula nawe komweko. Ndipo pamenepo ndidzakomana ndi ana a Israele; ndipo chihema chidzapatulidwa ndi ulemerero wanga. Ndipo ndidzapatula chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe; ndidzapatulanso Aroni ndi ana ake amuna omwe, andichitire ntchito ya nsembe. Ndipo ndidzakhala pakati pa ana a Israele, ndi kukhala Mulungu wao. Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, amene ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito, kuti ndikhale pakati pao. Ine ndine Yehova Mulungu wao. Ndipo upange guwa la nsembe la kufukizapo; ulipange la mtengo wakasiya. Utali wake ukhale mkono, ndi kupingasa kwake mkono; likhale laphwamphwa; ndi msinkhu wake mikono iwiri; nyanga zake zituluke m'mwemo. Ndipo ulikute ndi golide woona, pamwamba pake ndi mbali zake zozungulira, ndi nyanga zake; ulipangirenso mkombero wagolide pozungulira. Ndipo ulipangire mphete ziwiri zagolide pansi pa mkombero wake; uziike pa nthiti zake ziwiri, pa mbali zake ziwiri; zikhale zopisamo mphiko kulinyamula nazo. Ndipo upange mphiko za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi golide. Nuliike chakuno cha nsalu yotchinga ili ku likasa la mboni, patsogolo pa chotetezerapo chili pamwamba pa mboni, pomwe ndidzakomana ndi iwe. Ndipo Aroni azifukizapo chofukiza cha zonunkhira zokoma m'mawa ndi m'mawa, pamene akonza nyalizo, achifukize. Ndipo pamene Aroni ayatsa nyalizo madzulo, achifukize chofukiza chosatha pamaso pa Yehova mwa mibadwo yanu. Musafukizapo chofukiza chachilendo, kapena nsembe yopsereza, kapena nsembe yaufa; musathirepo nsembe yothira. Ndipo Aroni azichita choteteza pa nyanga zake kamodzi m'chaka; alichitire choteteza ndi mwazi wa nsembe yauchimo ya choteteza, mwa mibadwo yanu; ndilo lopatulika kwambiri la Yehova. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Pamene uwerenga ana a Israele, monga mwa mawerengedwe ao, munthu yense apereke kwa Yehova chiombolo cha pa moyo wake, pa kuwerengedwa iwowa; kuti pasakhale mliri pakati pao, pakuwerengedwa iwowa. Ichi achipereke, yense wakupita kwa owerengedwa; limodzi la magawo awiri a sekeli, monga sekeli la malo opatulika; (sekeli ndilo magera makumi awiri,) limodzi la magawo awiri a sekeli, ndilo chopereka cha Yehova. Yense wakupita kwa owerengedwawo, wa zaka makumi awiri ndi wa mphambu zake, apereke choperekacho kwa Yehova. Wachuma asachulukitsepo, ndi osauka asachepse pa limodzi mwa magawo awiri a sekeli, pakupereka chopereka kwa Yehova, kuchita choteteza cha miyoyo yanu. Ndipo uzilandira ndalama za choteteza kwa ana a Israele, ndi kuzipereka pa ntchito ya chihema chokomanako; kuti zikhale chikumbutso cha ana a Israele pamaso pa Yehova, kuchita choteteza cha miyoyo yanu. Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, ndi kuti, Upangenso mkhate wamkuwa, ndi tsinde lake lamkuwa, wakusambiramo; nuuike pakati pa chihema chokomanako ndi guwa la nsembe, ndi kuthiramo madzi. Ndipo Aroni ndi ana ake amuna azisambiramo manja ao ndi mapazi ao; pakulowa iwo m'chihema chokomanako asambe ndi madzi, kuti angafe; kapena poyandikiza guwa la nsembe kutumikirako, kufukiza nsembe yamoto ya Yehova; asambe manja ao ndi mapazi ao, kuti angafe: liwakhalire lemba losatha, kwa iye ndi kwa mbeu zake, mwa mibadwo yao. Yehova ananenanso ndi Mose, ndi kuti, Udzitengerenso zonunkhira zomveka, mure woyenda masekeli mazana asanu ndi sinamoni wonunkhira wa limodzi la magawo awiri a mureyo, ndilo masekeli mazana awiri kudza makumi asanu, ndi nzimbe zonunkhira mazana awiri kudza makumi asanu, ndi kida mazana asanu, monga sekeli la malo opatulika, ndi mafuta a azitona hini limodzi; ndipo ukonze nazo mafuta odzoza opatulika, osanganizika monga mwa machitidwe a wosanganiza; akhale mafuta odzoza opatulika. Ndipo udzoze nao chihema chokomanako, ndi likasa la mboni, ndi gomelo ndi zipangizo zake zonse, ndi choikapo nyali ndi zipangizo zake, ndi guwa la nsembe lofukizapo, ndi guwa la nsembe yopsereza ndi zipangizo zake zonse, ndi mkhate wosambiramo ndi tsinde lake. Ndipo uzipatule, kuti zikhale zopatulika ndithu; zonse zakuzikhudza zidzakhala zopatulika. Ndipo udzoze Aroni ndi ana ake amuna, ndi kuwapatula andichitire ntchito ya nsembe. Nulankhule ndi ana a Israele, ndi kuti, Awa ndi mafuta odzoza opatulika a Ine mwa mibadwo yanu. Asawatsanulire pa thupi la munthu; kapena musakonza ena onga awa, mwa makonzedwe ake; awa ndiwo opatulika, muwayese opatulika. Aliyense amene akonza ena otere, kapena aliyense awaika pa mlendo, ameneyo asazidwe kwa anthu a mtundu wake. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Udzitengere zonunkhira, natafi, ndi sekeleti, ndi kelebuna; zonunkhira pamodzi ndi lubani loona; miyeso yofanana; ndipo uzikonza nazo chofukiza, chosanganiza mwa machitidwe a wosanganiza, chokometsera ndi mchere, choona, chopatulika; nupere china chisalale, nuchiike chakuno cha mboni m'chihema chokomanako, kumene ndidzakomana ndi iwe; uchiyese chopatulika ndithu. Koma za chofukizacho uchikonze, musadzikonzere nokha china, mwa makonzedwe ake amene; muchiyese chopatulika cha Yehova. Aliyense wokonza china chotere kununkhizapo, asadzidwe kwa anthu a mtundu wake. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Taona ndaitana ndi kumtchula dzina lake, Bezalele, mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda; ndipo ndamdzaza ndi mzimu wa Mulungu, ndi luso, ndi nzeru, ndi chidziwitso, ndi m'ntchito zilizonse, kulingirira ntchito zaluso, kuchita ndi golide ndi siliva ndi mkuwa, ndi kuzokota miyala yoikika, ndi kozokota mtengo, kuchita ntchito zilizonse. Ndipo Ine, taona, ndampatsa Oholiyabu, mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani, akhale naye; ndipo ndaika luso m'mitima ya onse a mtima waluso, kuti apange zonse ndakuuza iwe; chihema chokomanako, likasa la mboni, ndi chotetezerapo chili pamwamba pake, ndi zipangizo zonse za chihemacho; ndi gomelo ndi zipangizo zake, ndi choikapo nyali choona ndi zipangizo zake, ndi guwa la nsembe lofukizapo; ndi guwa la nsembe yopsereza ndi zipangizo zake zonse, ndi mkhate ndi tsinde lake; ndi zovala zotumikira nazo, ndi zovala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zovala za ana ake, zakuchita nazo ntchito ya nsembe; ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza cha zonunkhira zokoma za malo opatulika; azichita monga mwa zonse ndakuuza iwe. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Koma iwe, lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Muzisunga masabata anga ndithu; pakuti ndiwo chizindikiro pakati pa Ine ndi inu mwa mibadwo yanu; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova wakukupatulani. Ndipo muzisunga Sabata; popeza ndilo lopatulika la kwa inu; aliyense wakuliipsa aphedwe ndithu; pakuti aliyense wakugwira ntchito m'mwemo, munthu ameneyo asadzidwe mwa anthu a mtundu wake. Agwire ntchito masiku asanu ndi limodzi; koma lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata lakupumula, lopatulika la Yehova; aliyense wogwira ntchito tsiku la Sabata aphedwe ndithu. Chifukwa chake ana a Israele azisunga Sabata, kuchita Sabata mwa mibadwo yao, likhale pangano losatha; ndicho chizindikiro chosatha pakati pa Ine ndi ana a Israele; pakuti Yehova analenga zam'mwamba ndi dziko lapansi masiku asanu ndi limodzi, napumula tsiku lachisanu ndi chiwiri, naonanso mphamvu. Ndipo atatha Iye kulankhula ndi Mose, pa phiri la Sinai, anampatsa magome awiri a mboni, magome amiyala, olembedwa ndi chala cha Mulungu. Koma pamene anaona kuti Mose anachedwa kutsika m'phiri, anthuwo anasonkhana kwa Aroni, nanena naye, Ukani, tipangireni milungu yakutitsogolera; pakuti Mose uyu, munthuyu anatikweza kuchokera m'dziko la Ejipito, sitidziwa chomwe chamgwera. Ndipo Aroni ananena nao, Thyolani mphete zagolide zili m'makutu a akazi anu, a ana anu aamuna ndi aakazi, ndi kubwera nazo kwa ine. Ndipo anthu onse anathyola mphete zagolide zinali m'makutu mwao, nabwera nazo kwa Aroni Ndipo anazilandira ku manja ao, nachikonza ndi chozokotera, nachiyenga mwanawang'ombe; ndipo anati, Siyi milungu yako, Israele, imene inakukweza kuchokera m'dziko la Ejipito. Pakuchiona Aroni, anamanga guwa la nsembe patsogolo pake; ndipo Aroni anafuula nati, Mawa aliko madyerero a Yehova. Ndipo m'mawa mwake anauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, nabwera nazo nsembe zamtendere; ndi anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nauka kusewera. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, tsikatu, pakuti anthu ako udakwera nao kuchokera m'dziko la Ejipito wadziipsa; wapatuka msanga njira imene ndinawauza; wadzinyengera mwanawang'ombe, namgwadira, namphera nsembe, nati, Siyi milungu yako, Israele, imene inakukweza kuchokera m'dziko la Ejipito. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ndawapenya anthu awa, taona, ndiwo anthu opulupudza; ndipo tsopano ndileke, kuti ndipse mtima pa awo ndi kuwatha, ndi kukuza iwe ukhale mtundu waukulu. Ndipo Mose anapemba kwa Yehova Mulungu wake, nati, Yehova, mtima wanu upserenji pa anthu anu, amene munawatulutsa m'dziko la Ejipito ndi mphamvu yaikulu, ndi dzanja lolimba? Akaneneranji Aejipito, ndi kuti, Anawatulutsa choipa, kuti awaphe m'mapiri, ndi kuwatha pankhope pa dziko lapansi? Pepani, lekani choipacho cha pa anthu anu. Kumbukirani Abrahamu, Isaki ndi Israele, atumiki anu, amene munawalumbirira ndi kudzitchula nokha, amene munanena nao, Ndidzachulukitsa mbeu zanu ngati nyenyezi za kuthambo, ndi dziko ili lonse ndanenali ndidzapatsa mbeu zanu, likhale cholowa chao nthawi zonse. Ndipo Yehova analeka choipa adanenachi, kuwachitira anthu ake. Ndipo Mose anatembenuka, natsika m'phirimo, magome awiri a mboni ali m'dzanja lake; magome olembedwa kwina ndi kwina; analembedwa mbali ina ndi inzake yomwe. Ndipo magomewo ndiwo ntchito ya Mulungu, kulembaku ndiko kulemba kwa Mulungu, kozokoteka pa magomewo. Ndipo pamene Yoswa anamva phokoso la kufuula kwa anthu, anati kwa Mose, Kuli phokoso la nkhondo kuchigono. Koma iye anati, Phokosoli sindilo la kufuula kwa olakika, kapena la kufuula kwa opasuka; koma phokoso ndikumvali ndilo la othirirana mang'ombe. Ndipo kunali, pamene anayandikiza chigono, anaona mwanawang'ombeyo ndi kuvinako; ndipo Mose anapsa mtima, nataya magome ali m'manja mwake, nawaswa m'tsinde mwa phiri. Ndipo anatenga mwanawang'ombe anampangayo, namtentha ndi moto, nampera asalale, namwaza pamadzi, namwetsako ana a Israele. Ndipo Mose anati kwa Aroni, Anthu awa anakuchitiranji, kuti iwe watengera iwo kulakwa kwakukulu kotere? Ndipo Aroni anati, Asapse mtima mbuye wanga; udziwa anthuwa kuti akhumba choipa. Pakuti ananena nane, Tipangireni milungu yakutitsogolera; popeza Mose uyu, munthuyu anatikweza kuchokera m'dziko la Ejipito, sitidziwa chomwe chamgwera. Ndipo ndinanena nao, Aliyense ali naye golide amthyole; ndipo anandipatsa; ndipo ndinachiponya m'moto, ndimo anatulukamo mwanawang'ombe uyu. Ndipo pamene Mose anaona kuti anthu anamasuka, popeza Aroni adawamasula kuti awatonze adani ao, Mose anaima pa chipata cha chigono, nati, Onse akuvomereza Yehova, adze kwa ine. Pamenepo ana amuna onse a Levi anasonkhana kwa iye. Ndipo ananena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Yense amange lupanga lake m'chuuno mwake, napite, nabwerere kuyambira chipata kufikira chipata, pakati pa chigono, naphe yense mbale wake, ndi yense bwenzi lake, ndi yense mnansi wake. Ndipo ana a Levi anachita monga mwa mau a Mose; ndipo adagwa tsiku lija anthu ngati zikwi zitatu. Popeza Mose adati, Mdzazireni Yehova manja anu lero, pakuti yense akhale mdani wa mwana wake wamwamuna, ndi mdani wa mbale wake; kuti akudalitseni lero lino. Ndipo kunali m'mawa mwake, kuti Mose anati kwa anthu, Mwachimwa kuchimwa kwakukulu; koma ndikwera kwa Yehova tsopano, kapena ndidzachita chotetezera uchimo wanu. Ndipo Mose anabwerera kunka kwa Yehova, nati, Ha! Pepani, anthu awa anachimwa kuchimwa kwakukulu, nadzipangira milungu yagolide. Koma tsopano, kapena mudzakhululukira kuchimwa kwao; koma ngati mukana, mundifafanizetu, kundichotsa m'buku lanu limene munalembera, Ndipo Yehova anati kwa Mose, Iye amene wandichimwira, ndifafaniza yemweyo kumchotsa m'buku langa. Ndipo tsopano, muka, tsogolera anthu kunka nao kumene ndinakuuza; taona, mthenga wanga akutsogolera; koma tsiku lakuwazonda Ine ndidzawalanga chifukwa cha kuchimwa kwao. Ndipo Yehova anakantha anthu, chifukwa anapanga mwanawang'ombe amene Aroni anapanga. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, kwera kuchokera kuno, iwe ndi anthu amene unawakweza kuchokera m'dziko la Ejipito, kunka ku dzikolo ndinalumbirira nalo Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, ndi kuti, Ndidzapatsa mbeu zako ilo; ndipo ndidzatuma mthenga akutsogolere; ndipo ndidzapirikitsa Akanani, ndi Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi; kudziko koyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, pakuti sindidzakwera pakati pa inu; popeza inu ndinu anthu opulupudza; ndingathe inu panjira. Ndipo pamene anthu anamva mau awa oipa anachita chisoni; ndipo panalibe mmodzi anavala zokometsera zake. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi ana a Israele, Inu ndinu anthu opulupudza; ndikakwera kulowa pakati pa inu kamphindi kamodzi, ndidzakuthani; koma tsopano, vulani zokometsera zanu, kuti ndidziwe chomwe ndikuchitireni. Ndipo ana a Israele anazichotsera zokometsera zao kuyambira pa phiri la Horebu. Ndipo Mose akatenga chihemacho nachimanga kunja kwa chigono, kutali kwa chigono; nachitcha, Chihema chokomanako. Ndipo kunakhala kuti yense wakufuna Yehova anatuluka kunka ku chihema chokomanako kunja kwa chigono. Ndipo kunali, pakutuluka Mose kunka ku chihemacho kuti anthu onse anaimirira, nakhala chilili, munthu yense pakhomo pa hema wake, nachita chidwi pa Mose, kufikira atalowa m'chihemacho. Ndipo kunali, pakulowa Mose m'chihemacho, mtambo njo udafutsika, nuima pakhomo pa chihemacho; ndipo Yehova analankhula ndi Mose. Ndipo anthu onse anaona mtambo njo ulikuima pakhomo pa chihema; ndi anthu onse anaimirira, nalambira, yense pakhomo pa hema wake. Ndipo Yehova ananena ndi Mose kopenyana maso, monga munthu alankhula ndi bwenzi lake. Ndipo anabwerera kunka kuchigono; koma mtumiki wake Yoswa mwana wa Nuni, ndiye mnyamata msinkhu wake, sanachoke m'chihemamo. Ndipo Mose anati kwa Yehova, Taonani, Inu munena ndi ine, Kwera nao anthu awa; koma simunandidziwitsa amene mudzamtuma amuke nane. Koma munati, Ndikudziwa dzina lako, wapezanso ufulu pamaso panga. Ndipo tsopano, ngati ndapeza ufulu pamaso panu, mundidziwitsetu njira zanu, kuti ndikudziweni, ndi kuti ndipeze ufulu pamaso panu; ndipo penyani kuti mtundu uwu ndi anthu anu. Ndipo anati, Nkhope yanga idzamuka nawe, ndipo ndidzakupumuza. Ndipo ananena ndi Iye, Ikapanda kumuka nane nkhope yanu, musatikweze kuchokera kuno. Pakuti chidziwika ndi chiyani tsopano kuti ndapeza ufulu pamaso panu, ine ndi anthu anu? Si pakumuka nafe Inu, kuti ine ndi anthu anu tisiyane ndi anthu onse akukhala pa nkhope ya dziko lapansi? Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ichi chomwe wanenachi ndidzachita; pakuti wapeza ufulu pamaso panga, ndipo ndikudziwa dzina lako. Ndipo anati, Ndionetsenitu ulemerero wanu. Ndipo Iye anati, Ndidzapititsa ukoma wanga wonse pamaso pako, ndipo ndidzatchula dzina la Yehova pamaso pako; ndipo ndidzachitira ufulu amene ndidzamchitira ufulu; ndi kuchitira chifundo amene ndidzamchitira chifundo. Ananenanso, Sungathe kuona nkhope yanga; pakuti palibe munthu adzandiona Ine ndi kukhala ndi moyo. Ndipo Yehova anati, Taona pali Inepo pali malo, ndipo uime pathanthwe; ndipo kudzakhala, pakupitira ulemerero wanga, ndidzakuika mu mpata wa thanthwe, ndi kukuphimba ndi dzanja langa, mpaka nditapitirira; ndipo pamene ndichotsa dzanja langa udzaona m'mbuyo mwanga; koma nkhope yanga siidzaoneka. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Dzisemere magome awiri amiyala onga oyamba aja; ndipo ndidzalembera pa magomewo mau omwewo anali pa magome oyambawo, amene unawaswa. Nukonzekeretu m'mawa, nukwere m'mawa m'phiri la Sinai, nuimepo pamaso panga pamwamba pa phiri. Palibe munthu akwere ndi iwe, asaonekenso munthu aliyense m'phiri monse; ndi zoweta zazing'ono kapena zoweta zazikulu zisadye kuphiri kuno. Ndipo anasema magome awiri a miyala, onga oyamba aja; ndipo Mose anauka mamawa nakwera m'phiri la Sinai, monga Yehova adamuuza, nagwira m'dzanja mwake magome awiri amiyala. Ndipo Yehova anatsika mumtambo, naimapo pamodzi ndi iye, nafuula dzina la Yehova. Ndipo Yehova anapita pamaso pake, nafuula, Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi; wakusungira anthu osawerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa; koma wosamasula wopalamula; wakulangira ana ndi zidzukulu chifukwa cha mphulupulu ya atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai. Ndipo Mose anafulumira, naweramira pansi nalambira. Ndipo anati, Ngati ndapeza ufulu tsopano pamaso panu, Ambuye, ayendetu Ambuye pakati pa ife; pakuti awa ndi anthu opulupudza; ndipo mutikhululukire mphulupulu ndi uchimo wathu, ndipo mutilandire tikhale cholowa chanu. Ndipo Iye anati, Taona, Ine ndichita pangano; ndidzachita zozizwa pamaso pa anthu ako onse, sizinachitika zotere ku dziko lonse lapansi, kapena ku mtundu uliwonse wa anthu; ndipo anthu onse amene uli pakati pao adzaona ntchito ya Yehova, pakuti chinthu ndikuchitirachi nchoopsa. Dzisungire chimene Ine ndikuuza lero lino: taona, ndiingitsa pamaso pako Aamori ndi Akanani, ndi Ahiti ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi. Dzichenjere ungachite pangano ndi anthu a ku dziko limene umukako, lingakhale msampha pakati panu; koma mupasule maguwa a nsembe ao, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kulikha zifanizo zao; pakuti musalambira mulungu wina; popeza Yehova dzina lake ndiye Wansanje, ali Mulungu wansanje; ungachite pangano ndi iwo okhala m'dzikomo; ndipo angachite chigololo pakutsata milungu yao, nangaphere nsembe milungu yao, ndipo angakuitane wina, nukadye naye nsembe zake; ndipo ungatengereko ana ako amuna ana ao akazi; nangachite chigololo ana ao akazi potsata milungu yao, ndi kuchititsa ana anu amuna chigololo potsata milungu yao. Usadzipangire milungu yoyenga. Uzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa. Uzidya mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri, monga ndakuuza pa nthawi yonenedwa, m'mwezi wa Abibu; pakuti mwezi wa Abibu unatuluka m'Ejipito. Onse oyambira kubadwa ndi anga; ndi zoweta zanu zonse zazimuna, zoyamba za ng'ombe ndi za nkhosa. Koma woyamba wa bulu uzimuombola ndi mwanawankhosa; ukapanda kumuombola, uzimthyola khosi. Ana anu amuna oyamba onse uziwaombola. Ndipo asamaoneka pamaso panga opanda kanthu. Masiku asanu ndi limodzi uzigwira ntchito, koma lachisanu ndi chiwiri uzipumula; nyengo yakulima ndi nyengo yamasika uzipumula. Ndipo uzichita chikondwerero cha Masabata, ndicho chikondwerero cha Zipatso zoyamba za Masika a tirigu, ndi chikondwerero cha Kututa pakutha pa chaka. Amuna ako onse azioneka pamaso pa Yehova Mulungu, Mulungu wa Israele, katatu chaka chimodzi. Pakuti ndidzaingitsa mitundu ya anthu pamaso pako, ndi kukulitsa malire ako; ndipo palibe munthu adzakhumba dziko lako, pakukwera iwe kudzaoneka pamaso pa Yehova Mulungu wako katatu chaka chimodzi. Usapereke mwazi wa nsembe yanga yophera pamodzi ndi mkate wachotupitsa; ndi nsembe yophera ya chikondwerero cha Paska asaisiye kufikira m'mawa. Uzibwera nazo zipatso zoyambayamba za nthaka yako kunyumba ya Yehova Mulungu wako. Usaphika mwanawambuzi mu mkaka wa make. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ulembere mau awa; pakuti monga mwa mau awa ndapangana ndi iwe ndi Israele. Ndipo anakhala pomwepo ndi Yehova masiku makumi anai, usana ndi usiku; sanadye mkate kapena kumwa madzi. Ndipo analembera pa magomewo mau a panganolo, mau khumiwo. Ndipo kunali pakutsika Mose pa phiri la Sinai, ndi magome awiri a mboni m'dzanja lake la Mose, pakutsika iye m'phirimo, Mose sanadziwe kuti khungu la nkhope yake linanyezimira popeza Iye adalankhula naye. Ndipo pamene Aroni ndi ana onse a Israele anaona Mose, taonani, khungu la nkhope yake linanyezimira; ndipo anaopa kumyandikiza. Koma Mose anawaitana; ndipo Aroni ndi akazembe onse a khamu la anthu anabwera kwa iye; ndipo Mose analankhula nao. Ndipo atatero, ana onse a Israele anayandikiza; ndipo iye anawauza zonse Yehova adalankhula naye m'phiri la Sinai. Ndipo Mose atatha kulankhula nao, anaika chophimba pankhope pake. Koma pakulowa Mose pamaso pa Yehova kunena ndi Iye, anachotsa chophimbacho, kufikira akatuluka; ndipo atatuluka analankhula ndi ana a Israele chimene adamuuza. Ndipo ana a Israele anaona nkhope ya Mose, kuti khungu la nkhope ya Mose linanyezimira; ndipo Mose anaikanso chophimba pankhope pake, kufikira akalowa kulankhula ndi Iye. Ndipo Mose anasonkhanitsa khamu lonse la ana a Israele, nanena nao, Siwa mau amene Yehova anauza, kuti muwachite. Masiku asanu ndi limodzi azigwira ntchito, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri muliyese lopatulika, Sabata lakupuma la Yehova: aliyense agwira ntchito pamenepo, aphedwe. Musamasonkha moto m'nyumba zanu zilizonse tsiku la Sabata. Ndipo Mose ananena ndi khamu lonse la ana a Israele, ndi kuti, Ichi ndi chimene Yehova anauza ndi kuti, Mumtengere Yehova chopereka cha mwa zanu; aliyense wa mtima womfunitsa mwini abwere nacho, ndicho chopereka cha Yehova; golide, ndi siliva, ndi mkuwa; ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ubweya wa mbuzi; ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, ndi mtengo wakasiya; ndi mafuta akuunikira, ndi zonunkhira za mafuta odzoza, ndi chofukiza cha fungo lokoma; ndi miyala yasohamu, ndi miyala yoika ya efodi, ndi ya chapachifuwa. Ndipo abwere yense wa mtima waluso mwa inu, napange zonse zimene Yehova anauza; Kachisi, hema wake, ndi chophimba chake, zokowera zake, ndi matabwa ake, mitanda yake, mizati, nsanamira, ndi nsichi zake, ndi makamwa ao; likasa, ndi mphiko zake, chotetezerapo, ndi nsalu yotchinga yotseka; gome, ndi mphiko zake, ndi zipangizo zake zonse, ndi mkate woonekera; ndi choikapo nyali cha kuunika, ndi zipangizo zake, ndi nyali zake, ndi mafuta a kuunika; ndi guwa la nsembe lofukizapo, ndi mphiko zake, ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza cha fungo lokoma, ndi nsalu yotsekera pakhomo, pa khomo la Kachisi; guwa la nsembe yopsereza, ndi sefa wamkuwa, mphiko zake, ndi zipangizo zake zonse, mkhate ndi tsinde lake; nsalu zochingira za kubwalo, nsichi zake, ndi makamwa ake, ndi nsalu yotsekera ku chipata cha pabwalo; zichiri za chihema, ndi zichiri za kubwalo, ndi zingwe zao; zovala za kutumikira nazo m'malo opatulika, zovala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zovala za ana ake, zakugwira nazo ntchito ya nsembe. Ndipo khamu lonse la ana a Israele linachoka pamaso pa Mose. Ndipo anadza, aliyense wofulumidwa mtima, ndi yense mzimu wake wamfunitsa, nabwera nacho chopereka cha Yehova, cha ku ntchito ya chihema chokomanako, ndi ku utumiki wake wonse, ndi ku zovala zopatulika. Ndipo anadza amuna ndi akazi, onse akufuna mtima eni ake, nabwera nazo mphete za mphuno, mphete za m'makutu, ndi mphete zosindikizira, ndi zigwinjiri, zonsezi zokometsera za golide; inde yense wakupereka kwa Yehova chopereka chagolide. Ndipo aliyense kwao kunapezeka lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ubweya wa mbuzi, ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, anabwera nazo. Yense wakupereka chopereka cha siliva ndi mkuwa, anabwera nacho chopereka cha Yehova; ndi yense amene kwao kunapezeka mtengo wakasiya wa ku machitidwe onse a ntchitoyi, anabwera nao. Ndi akazi onse a mtima waluso anapota ndi manja ao, nabwera nalo thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa. Ndi akazi onse ofulumidwa mtima ndi luso anapota ubweyawo wa mbuzi. Ndi akulu anabwera nayo miyala yasohamu, ndi miyala yoti aiike kuefodi, ndi kuchapachifuwa; ndi zonunkhira, ndi mafuta akuunikira, ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza za fungo lokoma. Amuna ndi akazi onse a ana a Israele amene mitima yao inawafunitsa eni kubwera nazo za ku ntchito yonse imene Yehova anauza ipangike ndi dzanja la Mose, anabwera nacho chopereka chaufulu, kuchipereka kwa Yehova. Ndipo Mose anati kwa ana a Israele, Taonani, Yehova anaitana, ndi kumtchula dzina lake, Bezalele, mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda; ndipo anamdzaza ndi mzimu wa Mulungu, ndi luso, ndi nzeru, ndi chidziwitso, za m'ntchito zilizonse; kulingirira ntchito zaluso, kuchita ndi golide, ndi siliva, ndi mkuwa; ndi kuzokota miyala yoikika, ndi kuzokota mitengo, kuchita m'ntchito zilizonse zaluso. Ndipo anaika m'mtima mwake kuti alangize ena, iye ndi Oholiyabu mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani. Amenewo anawadzaza ndi luso lamtima, lakuchita ntchito zilizonse, ya kuzokota miyala, ndi ya mmisiri waluso, ndi ya wopikula ndi lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ya muomba, ya iwo akuchita ntchito iliyonse, ndi ya iwo olingirira ntchito yaluso. Pamenepo anachita Bezalele ndi Oholiyabu, ndi anthu aluso, amene Yehova adaika luso ndi nzeru m'mtima mwao adziwe machitidwe ake a ntchito yonse ya utumiki wake wa malo opatulika, monga mwa zonse adauza Yehova. Ndipo Mose adaitana Bezalele ndi Oholiyabu, ndi anthu onse aluso, amene Yehova adaika luso m'mtima mwao, onse ofulumidwa mtima ayandikize kuntchito kuichita. Ndipo analandira kwa Mose chopereka chonse, chimene ana a Israele adabwera nacho chikhale cha machitidwe a ntchito ya malo opatulika, aipange nacho. Koma anaonjeza kubwera nazo kwa iye zopereka zaufulu, m'mawa ndi m'mawa. Ndipo aluso onse, akuchita ntchito yonse ya malo opatulika, anadza onse ndi kusiya ntchito yao analinkuchita; nanena ndi Mose, ndi kuti, Anthu alinkubwera nazo zochuluka, zakuposera zoyenera ntchito imene Yehova anauza ichitike. Ndipo Mose analamulira, ndipo anamveketsa mau mwa chigono chonse, ndi kuti, Asaonjezere ntchito ya ku chopereka cha malo opatulika, ngakhale mwamuna ngakhale mkazi. Tero anawaletsa anthu asabwere nazo zina. Popeza zipangizo zinakwanira ntchito yonse ichitike, zinatsalakonso. Ndipo onse a mtima waluso mwa iwo akuchita ntchitoyi anapanga Kachisi ndi nsalu zophimba khumi; anaziomba ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi akerubi, ntchito ya mmisiri. Utali wake wa nsalu yophimba imodzi ndiwo mikono makumi awiri kudza isanu ndi itatu, ndi kupingasa kwake kwa nsalu imodzi mikono inai; nsalu zonse zinafanana muyeso wao. Ndipo analumikiza nsalu zisanu ina ndi inzake; nalumikiza nsalu zisanu zina ina ndi inzake. Ndipo anaika magango ansalu yamadzi m'mphepete mwake mwa nsalu imodzi ku mkawo wa chilumikizano; nachita momwemo m'mphepete mwake mwa nsalu ya kuthungo, ya chilumikizano chachiwiri. Anaika magango makumi asanu pa nsalu imodzi, naikanso magango makumi asanu m'mphepete mwake mwa nsalu ya chilumikizano china; magango anakomanizana lina ndi linzake. Ndipo anazipanga zokowera makumi asanu zagolide, namanga nsalu pamodzi ndi zokowerazo; ndipo Kachisi anakhala mmodzi. Ndipo anaomba nsalu zophimba za ubweya wa mbuzi zikhale hema pamwamba pa Kachisi; anaomba nsalu zophimba khumi ndi imodzi. Utali wake wa nsalu imodzi ndiwo mikono makumi atatu, ndi kupingasa kwake kwa nsalu imodzi ndiko mikono inai; nsalu khumi ndi imodzi zinafanana muyeso wao. Ndipo anamanga pamodzi nsalu zisanu pa zokha, ndi nsalu zisanu ndi imodzi pa zokha. Ndipo anapanga magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu imodzi, ya kuthungo, ya chilumikizano, naika magango makumi asanu m'mphepete mwa nsalu ya kuthungo, ya chilumikizano china. Ndipo anapanga zokowera makumi asanu zamkuwa kumanga pamodzi hemalo, kuti likhale limodzi. Ndipo anasokera hemalo chophimba cha zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi chophimba cha zikopa za akatumbu pamwamba pake. Ndipo anapanga matabwa a Kachisi, oimirika, a mtengo wakasiya. Utali wake wa thabwa limodzi ndiwo mikono khumi, ndi kupingasa kwake kwa thabwa limodzi ndiko mkono ndi hafu. Pa thabwa limodzi panakhala mitsukwa iwiri, yomangika pamodzi; anawapanga momwemo matabwa onse a Kachisi. Ndipo anapanga matabwa a Kachisi; matabwa makumi awiri a ku mbali ya kumwera, kumwera; napanga makamwa makumi anai asiliva pansi pa matabwa makumi awiri; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi kwa mitsukwa yake iwiri, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina kwa mitsukwa yake iwiri. Ndi ku mbali ina ya Kachisi, mbali ya kumpoto, anapanga matabwa makumi awiri, ndi makamwa ao makumi anai asiliva; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina. Ndi ku mbali ya kumbuyo ya Kachisi kumadzulo anapanga matabwa asanu ndi limodzi. Anapanganso matabwa awiri a kungodya za Kachisi, m'mbali zake ziwiri. Ndipo anaphatikizika pamodzi patsinde, naphatikizika pamodzi pamutu pake ndi mphete imodzi; anatero nao onse awiri pangodya ziwiri. Ndipo panali matabwa asanu ndi atatu. Ndi makamwa ao asiliva, makamwa khumi kudza asanu ndi limodzi; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi. Ndipo anapanga mitanda ya mtengo wakasiya; isanu ya matabwa a pa mbali ina ya Kachisi, ndi mitanda isanu ya matabwa a pa mbali inzake ya Kachisi, ndi mitanda isanu ya matabwa a Kachisi ali pa mbali ya kumadzulo. Ndipo anapititsa mtanda wa pakatipo, pakati pa matabwa kufikira kuthungo. Ndipo anakuta matabwa ndi golide, napanga mphete zao zagolide zikhale zopisamo mitandayo, nakuta mitandayo ndi golide. Ndipo anaomba nsalu yotchinga ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; anachiomba ndi akerubi ntchito ya mmisiri. Ndipo anaipangira mizati inai ya kasiya, nazikuta ndi golide; zokowera zao zinali zagolide; ndipo anaziyengera makamwa anai asiliva. Ndipo anaomba nsalu yotsekera pa khomo la chihemacho, ya lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya wopikula; ndi nsanamira zake zisanu ndi zokowera zao; nakuta mitu yao ndi mitanda yao ndi golide; ndi makamwa ao asanu anali amkuwa. Ndipo Bezalele anapanga likasa la mtengo wakasiya; utali wake mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwake mkono ndi hafu, ndi msinkhu wake mkono ndi hafu; ndipo analikuta ndi golide woona m'kati ndi kunja, nalipangira mkombero wa golide pozungulira pake. Ndipo analiyengera mphete zinai zagolide pa miyendo yake inai; mphete ziwiri pa mbali yake imodzi, ndi mphete ziwiri pa mbali yake ina. Ndipo anapanga mphiko za mtengo wakasiya, nazikuta ndi golide. Ndipo anapisa mphiko m'mphetezo pa mbali zake za likasalo, kuti anyamulire nazo likasa. Ndipo anapanga chotetezerapo cha golide woona; utali wake mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwake mkono ndi hafu. Anapanganso akerubi awiri agolide; anachita kuwasula mapangidwe ake, pa mathungo ake awiri a chotetezerapo; kerubi mmodzi pa mbali yake imodzi, ndi kerubi wina pa mbali yake ina; anapanga akerubi ochokera m'chotetezerapo, pa mathungo ake awiri. Ndipo akerubi anafunyulira mapiko ao m'mwamba, ndi kuphimba chotetezerapo ndi mapiko ao, ndi nkhope zao zopenyana; zinapenya kuchotetezerapo nkhope zao. Ndipo anapanga gome la mtengo wakasiya; utali wake mikono iwiri, ndi kupingasa kwake mkono umodzi, ndi msinkhu wake mkono ndi hafu; ndipo analikuta ndi golide woona, nalipangira mkombero wagolide pozungulira pake. Analipangiranso mitanda pozungulirapo, yoyesa chikhato m'kupingasa kwake, ndi pamitanda pake pozungulira anapangirapo mkombero wagolide. Ndipo analiyengera mphete zinai zagolide, naika mphetezo pangodya zake zinai zokhala pa miyendo yake inai. Mphetezo zinali pafupi pa mitanda, zikhale zopisamo mphiko kunyamulira nazo gomelo. Ndipo anapanga mphiko za mtengo wakasiya, nazikuta ndi golide, kunyamulira nazo gomelo. Anapanganso zipangizo za gomelo, mbale zake, ndi zipande zake, ndi mitsuko yake, ndi zikho zake zakuthira nazo, za golide woona. Ndipo anapanga choikapo nyali cha golide woona; mapangidwe ake a choikapo nyalicho anachita chosula, tsinde lake ndi thupi lake, zikho zake, mitu yake, ndi maluwa ake zinakhala zochokera m'mwemo; ndi m'mbali zake munatuluka mphanda zisanu ndi imodzi; mphanda zitatu za choikapo nyali zotuluka m'mbali yake imodzi, ndi mphanda zitatu za choikapo nyali zotuluka m'mbali yake ina; pa mphanda imodzi panali zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi luwa; ndi pa mphanda ina zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi luwa zinatero mphanda zisanu ndi imodzi zotuluka m'choikapo nyali. Ndipo pa choikapo nyali chomwe panali zikho zinai zopangika ngati katungurume, mitu yake ndi maluwa ake; ndipo panali mutu pansi pa mphanda ziwiri, zotuluka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri, zotuluka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri, zotuluka m'mwemo, inatero pa mphanda zisanu ndi imodzi zochokera m'mwemo. Mitu yao ndi mphanda zao zinatuluka m'mwemo; chonsechi chinali chosulika pamodzi cha golide woona. Ndipo anapanga nyali zake zisanu ndi ziwiri ndi mbano zake, ndi zoolera zake, za golide woona. Anachipanga ichi ndi zipangizo zake zonse za talente wa golide woona. Ndipo anapanga guwa la nsembe lofukizapo la mtengo wakasiya; utali wake mkono, ndi kupingasa kwake mkono, laphwamphwa; ndi msinkhu wake mikono iwiri; nyanga zake zinatuluka m'mwemo. Ndipo analikuta ndi golide woona, pamwamba pake, ndi mbali zake pozungulira, ndi nyanga zake; ndipo analipangira mkombero wagolide pozungulira pake. Ndipo analipangira mphete ziwiri zagolide pansi pa mkombero wake, pangodya zake ziwiri, pa mbali zake ziwiri, zikhale zopisamo mphiko kulinyamulira nazo. Ndipo anazipanga mphiko za mtengo wakasiya, nazikuta ndi golide. Anapanganso mafuta opatulika akudzoza nao, ndi chofukiza choona cha fungo lokoma, mwa machitidwe a wosanganiza. Ndipo anapanga guwa la nsembe yopsereza la mtengo wakasiya; utali wake mikono isanu, ndi kupingasa kwake mikono isanu, laphwamphwa; ndi msinkhu wake mikono itatu. Ndipo anapanga nyanga zake pangodya zake zinai; nyanga zake zinakhala zotuluka m'mwemo; ndipo analikuta ndi mkuwa. Anapanganso zipangizo zonse za guwalo, zotayira, ndi zoolera, ndi mbale zowazira, ndi mitungo, ndi zopalira moto; zipangizo zake zonse anazipanga zamkuwa. Ndipo anapangira guwa la nsembelo sefa, malukidwe ake nja mkuwa, pansi pa khoma lamkati lake wakulekeza pakati pake. Ndipo anayengera mathungo anai a sefa wamkuwayo mphete zinai, zikhale zopisamo mphiko. Napanga mphiko za mtengo wakasiya, nazikuta ndi mkuwa. Ndipo anapisa mphikozo m'zimphetemo pa mbali za guwa la nsembe, kulinyamulira nazo; analipanga ndi matabwa, lagweregwere. Ndipo anapanga mkhate wamkuwa, ndi tsinde lake lamkuwa, wa akalirole a akazi otumikira, akutumikira pa khomo la chihema chokomanako. Ndipo anapanga bwalo; pa mbali ya kumwera, kumwera, nsalu zochingira za pabwalo zinali za bafuta wa thonje losansitsa, mikono zana limodzi; nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ao makumi awiri, amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zasiliva. Ndi pa mbali ya kumpoto mikono zana limodzi, nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ake makumi awiri, amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake yasiliva. Ndi pa mbali ya kumadzulo panali nsalu zochingira za mikono makumi asanu, nsichi zake khumi, ndi makamwa ake khumi; zokowera za nsichi ndi mitanda yake yasiliva. Ndi pa mbali ya kum'mawa, kum'mawa, mikono makumi asanu. Nsalu zochingira za pa mbali imodzi ya chipata nza mikono khumi ndi isanu; nsichi zake zitatu, ndi makamwa ake atatu; momwemonso pa mbali ina: pa mbali yino ndi pa mbali ina ya chipata cha pabwalo panali nsalu zochingira za mikono khumi ndi isanu; nsichi zake zitatu, ndi makamwa ake atatu. Nsalu zochingira zonse za pabwalo pozungulira zinali za bafuta wa thonje losansitsa. Ndipo makamwa a nsichi anali amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zasiliva; ndi zokutira mitu yake zasiliva; ndi nsichi zonse za pabwalo zinagwirana pamodzi ndi siliva. Ndi nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo ndiyo ntchito ya wopikula, ya lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; utali wake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake ndi kupingasa kwake mikono isanu, yolingana ndi nsalu zochingira za pabwalo. Ndi nsichi zake zinali zinai, ndi makamwa ake anai, amkuwa; zokowera zake zasiliva, ndi zokutira mitu yake ndi mitanda yake zasiliva. Ndi zichiri zonse za chihema, ndi za bwalo lake pozungulira, nza mkuwa. Ichi ndi chiwerengo cha zinthu za chihema, chihema cha mboni, monga anaziwerenga, monga mwa mau a Mose, achite nazo Alevi; anaziwerenga Itamara, mwana wa Aroni wansembe. Ndipo Bezalele mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda, anapanga zonse zimene Yehova adauza Mose. Ndi pamodzi naye Oholiyabu, mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani, ndiye wozokota miyala, ndi mmisiri waluso, ndiponso wopikula ndi lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa. Golide yense anachita naye mu ntchito yonse ya malo opatulika, golide wa choperekacho, ndicho matalente makumi awiri kudza asanu ndi anai, ndi masekeli mazana asanu ndi awiri, kudza makumi atatu, monga mwa sekeli wa malo opatulika. Ndipo siliva wa iwo owerengedwa a khamulo ndiwo matalente zana limodzi, ndi masekeli chikwi chimodzi, kudza mazana asanu ndi awiri, mphambu makumi asanu ndi awiri kudza asanu, kuyesa sekeli wa malo opatulika; Munthu mmodzi anapereka beka, ndiwo limodzi la magawo awiri la sekeli, kuyesa sekeli wa malo opatulika, anatero onse akupita kunka kwa owerengedwawo, kuyambira munthu wa zaka makumi awiri ndi oposa, ndiwo anthu zikwi mazana asanu ndi limodzi kudza zitatu, ndi mazana asanu mphambu makumi asanu. Ndipo matalente zana limodzi a siliva ndiwo a kuyengera makamwa a malo opatulika, ndi makamwa a nsalu yotchinga; makamwa zana limodzi matalente zana limodzi, talente limodzi kamwa limodzi. Ndipo anapanga zokowera za mizati nsanamira ndi nsichi ndi masekeli aja chikwi chimodzi kudza mazana asanu ndi awiri mphambu asanu, nakuta mitu yake, nazigwirizitsana pamodzi. Ndi mkuwa wa choperekacho ndiwo matalente makumi asanu ndi awiri, ndi masekeli zikwi ziwiri kudza mazana anai. Ndipo anapanga nao makamwa a pa khomo la chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe lamkuwa, ndi sefa wake amkuwa, ndi zipangizo zonse za guwa la nsembe, ndi makamwa a pabwalo pozungulira, ndi makamwa a ku chipata cha pabwalo, ndi zichiri zonse za chihema, ndi zichiri zonse za pabwalo pozungulira. Ndipo anaomba zovala zakutumikira nazo ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, atumikire nazo m'malo opatulika, naomba zovala zopatulika za Aroni; monga Yehova adamuuza Mose. Ndipo anaomba efodi wa golide, lamadzi, lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa. Ndipo anasula golide waphanthiphanthi, nalemba nsambo, kuti amuombe pamodzi ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya mmisiri. Anapangira efodi zapamapewa zolumikizana; pa nsonga ziwirizo anamlumikiza. Ndi mpango wa efodi wokhala pamenepo, wakummanga nao unali woombera kumodzi wa chiombedwe chomwechi; wa golide, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; monga Yehova adauza Mose. Ndipo anakonza miyala yasohamu, yogwirika m'zoikamo zagolide, yolocha ngati malochedwe a chosindikizira, ndi maina a ana a Israele. Ndipo anaiika pa zapamapewa za efodi, ikhale miyala ya chikumbutso kwa ana a Israele; monga Yehova adamuuza Mose. Ndipo anaomba chapachifuwa, ntchito ya mmisiri, monga maombedwe ake a efodi; cha golide, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa. Chinakhala chaphwamphwa; anachiomba chapachifuwa chopindika; utali wake dzanja limodzi, ndi kupingasa kwake dzanja limodzi, chinakhala chopindika. Ndipo anaika pomwepo mizere inai ya miyala; mzere wa odemu, pitida, ndi bareketi, ndiyo ya mzere woyamba. Ndi mzere wachiwiri wa nofeki, safiro, ndi yahalomu. Ndi mzere wachitatu wa lesemu, sibu, ndi akalama. Ndi mzere wachinai wa tarisisi, sohamu, ndi yasefe; inakhala yogwirika ndi golide maikidwe ake. Ndipo miyalayi inakhala monga mwa maina a ana a Israele, khumi ndi awiri, monga mwa maina ao; ngati malochedwe a chosindikizira, yonse monga mwa maina ake, kwa mafuko khumi ndi awiriwo. Ndipo anapangira pachapachifuwa maunyolo ngati zingwe, ntchito yopota ya golide woona. Anapanganso zoikamo ziwiri zagolide, ndi mphete ziwiri zagolide; naika mphete ziwirizo pa nsonga ziwiri za chapachifuwa. Ndipo anamanga maunyolo awiri opota agolide pa mphete ziwiri pa nsonga za chapachifuwa. Ndi nsonga zake ziwiri zina za maunyolo awiri opotawo anazimanga pa zoikamo ziwiri, nazimanga pa zapamapewa za efodi, m'tsogolo mwake. Ndipo anapanga mphete ziwiri zagolide, naziika pa nsonga ziwiri za chapachifuwa, m'mphepete mwake m'katimo, pa mbali ya kuefodi. Ndipo anapanga mphete ziwiri zagolide, naziika pa zapamapewa ziwiri za efodi pansi pake, pa mbali yake ya kutsogolo, pafupi pa msoko wake, pamwamba pa mpango wa efodi. Ndipo anamanga chapachifuwa pa mphete zake ndi mphete za efodi ndi mkuzi wamadzi, kuti chikhale pa mpango wa efodi, ndi kuti chapachifuwa chisamasuke paefodi; monga Yehova anamuuza Mose. Ndipo anaomba mwinjiro wa efodi, ntchito yoomba ya lamadzi lokha; ndi pakati pake polowa mutu, ngati polowa pa malaya ochingirizira, ndipo anabinyira pozungulira polowa pake, pangang'ambike. Napangira pa mkawo wa mwinjiro makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa. Ndipo anapanga miliu ya golide woona, napakiza miliu ndi makangaza, pa mkawo wa mwinjiro pozungulira, popakiza ndi makangaza. Mliu ndi khangaza, mliu ndi khangaza pa mkawo wa mwinjiro pozungulira, kutumikira nazo; monga Yehova anamuuza Mose. Ndipo anaomba malaya a bafuta, a ntchito yoomba, a Aroni, ndi a ana ake amuna, ndi nduwira yabafuta wa thonje losansitsa, ndi akapa okometsetsa a bafuta wa thonje losansitsa, ndi zovala za kumiyendo za bafuta wa thonje losansitsa, ndi mpango wabafuta wa thonje losansitsa, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ntchito ya wopikula; monga Yehova adamuuza Mose. Ndipo anapanga phanthiphanthi wa korona wopatulika wa golide woona, nalembapo lemba, ngati malochedwe a chosindikizira, KUPATULIKIRA YEHOVA. Namangako mkuzi wamadzi, kuumanga nao pamwamba pa nduwira; monga Yehova adamuuza Mose. Potero anatsiriza ntchito yonse ya Kachisi wa chihema chokomanako; ndipo ana a Israele adachita monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose, anachita momwemo. Ndipo anabwera naye Kachisi kwa Mose, chihemacho, ndi zipangizo zake zonse, zokowera zake, matabwa ake, mitanda yake, ndi mizati yake, nsanamira zake ndi nsichi zake, ndi makamwa ake; ndi chophimba cha zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi nsalu yotchinga yotsekera; likasa la mboni, ndi mphiko zake, ndi chotetezerapo; gomelo, zipangizo zake zonse, ndi mkate woonekera; choikapo nyali choona, nyali zake, ndizo nyali zimakonzekazi, ndi zipangizo zake zonse, ndi mafuta a kuunikira; ndi guwa la nsembe lagolide, ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza cha fungo lokoma, ndi nsalu yotsekera pa khomo la chihemacho; guwa la nsembe la mkuwa, ndi sefa wake wamkuwa, mphiko zake, ndi zipangizo zake zonse, mkhate ndi tsinde lake; nsalu zochingira za pabwalo, nsichi zake, ndi makamwa ake, ndi nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo, zingwe zake, ndi zichiri zake, ndi zipangizo zonse za ntchito ya Kachisi, za ku chihema chokomanako; zovala zokoma za kutumikira nazo m'malo opatulika, ndi zovala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zovala za ana ake, kuchita nazo ntchito ya nsembe. Monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose, momwemo ana a Israele anachita ntchito zonse. Ndipo Mose anaona ntchito zonse, ndipo, taonani, adaichita monga Yehova adamuuza, momwemo adachita. Ndipo Mose anawadalitsa. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Tsiku loyamba la mwezi woyamba ukautse Kachisi wa chihema chokomanako. Ndipo ukaikemo likasa la mboni, nuchinge likasalo ndi nsalu yotchingayo. Ulongenso gomelo, nukonzerepo zokonzera zake; ulongenso choikapo nyalicho, ndi kuyatsa nyali zake. Ndipo ukaike guwa la nsembe lofukizapo lagolide chakuno cha likasa la mboni, numange pa Kachisi nsalu yotsekera pakhomo. Ndipo ukaike guwa la nsembe yopsereza kunja kwa khomo la Kachisi wa chihema chokomanako. Ukaikenso mkhate pakati pa chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe, ndi kuthiramo madzi. Ndipo ukamange mpandawo pozungulira, ndi kupachika nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo. Pamenepo ukatenge mafuta odzoza, ndi kudzoza nao Kachisi, ndi zonse zili m'mwemo, ndi kumpatula, ndi zipangizo zake zonse; ndipo adzakhala wopatulika. Ndipo udzoze guwa la nsembe yopsereza, ndi zipangizo zake zonse, ndi kulipatula guwalo; ndipo guwalo lidzakhala lopatulika kwambiri. Udzozenso mkhate ndi tsinde lake, ndi kuupatula. Ndipo ubwere nao Aroni ndi ana ake amuna ku khomo la chihema chokomanako, ndi kuwasambitsa ndi madzi. Nuveke Aroni chovala zopatulikazo; ndi kumdzoza, ndi kumpatula andichitire Ine ntchito ya nsembe. Ndipo ubwere nao ana ake amuna ndi kuwaveka malaya am'kati; nuwadzoze, monga unadzoza atate wao, kuti andichitire ntchito ya nsembe; ndi kudzozedwa kwao kuwakhalire unsembe wosatha mwa mibadwo yao. Anatero Mose; monga mwa zonse Yehova adamuuza, momwemo anachita. Ndipo kunali, mwezi woyamba wa chaka chachiwiri, tsiku loyamba la mwezi, anautsa Kachisi, ndipo Mose anautsa Kachisi, nakhazika makamwa ake, naimika matabwa ake, namangapo mitanda yake, nautsa mizati ndi nsanamira zake. Ndipo anayalika hema pamwamba pa Kachisi, naika chophimba cha chihema pamwamba pake; monga Yehova adamuuza Mose. Ndipo anatenga mboniyo, naiika m'likasa, napisa mphiko palikasa, naika chotetezerapo pamwamba pa likasa; nalowa nalo likasa m'Kachisi, napachika nsalu yotchinga, natchinga likasa la mboni; monga Yehova adamuuza Mose. Ndipo anaika gomelo m'chihema chokomanako, pa mbali ya kumpoto ya Kachisi, kunja kwa nsalu yotchinga. Nakonzerapo mkate pamaso pa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose. Ndipo anaika choikapo nyali m'chihema chokomanako, popenyana ndi gome, pa mbali ya kumwera ya Kachisi. Nayatsa nyalizo pamaso pa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose. Ndipo anaika guwa la nsembe lagolide m'chihema chokomanako chakuno cha nsalu yotchinga; nafukizapo chofukiza cha fungo lokoma; monga Yehova adamuuza Mose. Ndipo anapachika ku Kachisi nsalu yotsekera pakhomo. Ndipo anaika guwa la nsembe yopsereza pa khomo la Kachisi wa chihema chokomanako, natenthapo nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa; monga Yehova adamuuza Mose. Ndipo anaika mkhate pakati pa chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe; nathiramo madzi osamba. Ndipo Mose ndi Aroni ndi ana ake amuna anasamba manja ao ndi mapazi ao m'menemo; pakulowa iwo m'chihema chokomanako, ndi pakuyandikiza guwa la nsembe anasamba; monga Yehova adamuuza Mose. Ndipo anautsa mpanda pozungulira pa chihema ndi guwa la nsembe, napachika nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo. Momwemo Mose anatsiriza ntchitoyi. Pamenepo mtambo unaphimba chihema chokomanako, ndi ulemerero wa Yehova unadzaza Kachisiyo. Ndipo Mose sanathe kulowa m'chihema chokomanako, popeza mtambo unakhalabe pamenepo; ndi ulemerero wa Yehova unadzaza Kachisi. Ndipo pakukwera mtambo kuchokera ku Kachisi, ana a Israele amayenda maulendo ao onse; koma ukapanda kukwera mtambo, samayenda ulendo wao kufikira tsiku loti wakwera. Pakuti mtambo wa Yehova unakhala pa Kachisi msana, ndi usiku munali moto m'menemo, pamaso pa mbumba yonse ya Israele, m'maulendo ao onse. Ndipo Yehova anaitana Mose, nanena naye ali m'chihema chokomanako Iye, nati, Lankhula ndi ana a Israele, nunene nao, Aliyense mwa inu akabwera nacho chopereka cha kwa Yehova, muzibwera nacho chopereka chanu chikhale cha zoweta, cha ng'ombe, kapena cha nkhosa, kapena cha mbuzi. Chopereka chake chikakhala nsembe yopsereza ya ng'ombe, azibwera nayo yaimuna yopanda chilema; abwere nayo ku khomo la chihema chokomanako, kuti alandirike pamaso pa Yehova. Ndipo aike dzanja lake pamutu pa nsembe yopsereza; ndipo idzalandiridwa m'malo mwake, imtetezere. Pamenepo aiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova; ndipo ana a Aroni, ansembewo, abwere nao mwazi, nawaze mwaziwo pozungulira pa guwa la nsembe, lokhala pa khoma la chihema chokomanako. Ndipo asende nsembe yopsereza, ndi kuikadzula ziwalo zake. Ndipo ana a Aroni wansembeyo asonkhe moto pa guwa la nsembe, ndi kukonza nkhuni pamotopo; ndi ana a Aroni, ansembewo, akonze ziwalozo, mutu, ndi mafuta pa nkhuni zili pa moto wa pa guwa la nsembe; koma atsuke ndi madzi matumbo ake ndi miyendo yake; ndi wansembe atenthe zonsezi pa guwa la nsembe, zikhale nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova. Ndipo chopereka chake chikakhala cha nkhosa, kapena cha mbuzi, chikhale nsembe yopsereza; azibwera nayo yaimuna yopanda chilema. Ndipo aiphere iyo pa mbali ya kumpoto ya guwa la nsembe, pamaso pa Yehova; ndipo ana a Aroni, ansembewo, awaze mwazi wake pa guwa la nsembe pozungulira. Ndipo aikadzule ziwalo zake, pamodzi ndi mutu wake ndi mafuta ake; ndi wansembeyo akonze izi pa nkhuni zili pa moto wa pa guwa la nsembe. Koma atsuke ndi madzi matumbo ndi miyendo; ndi wansembe abwere nazo zonse nazitenthe pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova. Ndipo chopereka chake cha kwa Yehova chikakhala nsembe yopsereza ya mbalame, azibwera nacho chopereka chake chikhale cha njiwa, kapena cha maunda. Ndipo wansembe abwere nacho ku guwa la nsembe, namwetule mutu wake, naitenthe pa guwa la nsembe; ndi mwazi wake aukamulire pa mbali ya guwa la nsembe, nachotse chitsokomero, ndi chipwidza chake, nazitaye kufupi kwa guwa la nsembe, kum'mawa, kudzala; nang'ambe mapiko ake osawachotsa konse ai; ndipo wansembeyo aitenthe pa guwa la nsembe, pa nkhuni zili pamoto; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova. Ndipo munthu akabwera nacho chopereka ndicho nsembe yaufa ya kwa Yehova, chopereka chake chizikhala cha ufa wosalala; ndipo athirepo mafuta, ndi kuikapo lubani. Ndipo abwere nayo kwa ana a Aroni, ansembewo; natengeko ufa, ndi mafuta odzala manja, ndi lubani wake wonse; ndipo wansembeyo aitenthe chikumbutso chake pa guwa la nsembe, ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova. Ndipo chotsalira cha nsembe yaufa chikhale cha Aroni ndi ana ake; ndicho chopatulika kwambiri cha nsembe zamoto za Yehova. Ndipo ukabwera nacho chopereka ndicho nsembe yaufa, yophika mumchembo, chizikhala cha timitanda ta ufa wosalala topanda chotupitsa tosanganiza ndi mafuta, kapena timitanda taphanthi topanda chotupitsa todzoza ndi mafuta. Ndipo nsembe yaufa yako ikakhala yokazinga m'chiwaya, ikhale ya ufa wosalala wopanda chotupitsa, wosanganiza ndi mafuta. Uphwanye, nuthirepo mafuta; ndiyo nsembe yaufa. Ndipo chopereka chako chikakhala nsembe yaufa ya mumphika, chikhale cha ufa wosalala ndi mafuta. Ndipo ubwere nayo nsembe yaufa yopangika ndi izi kwa Yehova; ndipo atabwera nacho kwa wansembe, iyeyo apite nacho ku guwa la nsembe. Ndipo wansembeyo atengeko chikumbutso pa nsembe yaufa, nachitenthe pa guwa la nsembe; ndicho nsembe yamoto ya fungo lokoma la kwa Yehova. Ndipo chotsalira cha nsembe yaufa chikhale cha Aroni ndi ana ake; ndicho chopatulika kwambiri cha nsembe zamoto za Yehova. Nsembe iliyonse yaufa, imene mubwera nayo kwa Yehova, isapangike ndi chotupitsa, pakuti musamatenthera Yehova nsembe yamoto yachotupitsa, kapena yauchi. Monga chopereka cha zipatso zoyamba muzipereka izi kwa Yehova: koma asazifukize pa guwa la nsembe zichite fungo lokoma. Ndipo chopereka chako chilichonse cha nsembe yaufa uzichikoleretsa ndi mchere; usasowe mchere wa chipangano cha Mulungu wako pa nsembe yako yaufa; pa zopereka zako zonse uzipereka mchere. Ndipo ukabwera nayo nsembe yaufa ya zipatso zoyamba kwa Yehova, uzibwera nayo nsembe yako ya zipatso zoyamba ikhale ya ngala zoyamba kucha, zoumika pamoto, zokonola. Ndipo uthirepo mafuta, ndi kuikapo lubani; ndiyo nsembe yaufa. Ndipo wansembe atenthe chikumbutso chake, atatapa pa tirigu wake wokonola, ndi pa mafuta ake, ndi kutenga lubani lake lonse; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova. Ndipo chopereka chake chikakhala nsembe yoyamika; akabwera nayo ng'ombe, kapena yaimuna kapena yaikazi, azibwera nayo yopanda chilema pamaso pa Yehova. Ndipo aike dzanja lake pa mutu wa chopereka chake, ndi kuipha pa chipata cha chihema chokomanako; ndipo ana a Aroni, ansembewo, awaze mwazi wake pa guwa la nsembe pozungulira. Pamenepo abwere nayo nsembe yamoto ya kwa Yehova, yotengako ku nsembe yoyamika; achotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo, ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pomwepo okhala m'chuuno, ndi chokuta cha mphafa chofikira kuimpso. Ndipo ana a Aroni azitenthe pa guwa la nsembe, pa nsembe yopsereza, ili pa nkhuni zimene zili pamoto; ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova. Ndipo chopereka chake chikakhala nkhosa kapena mbuzi, kuti ikhale nsembe yoyamika ya kwa Yehova; ingakhale yaimuna kapena yaikazi, azibwera nayo yopanda chilema; akabwera nayo nkhosa kuti ikhale chopereka chake, abwere nayo pamaso pa Yehova; naike dzanja lake pamutu pa chopereka chake, naiphe patsogolo pa chihema chokomanako; ndipo ana a Aroni awaze mwazi wake pa guwa la nsembe pozungulira. Pamenepo abwere nayo nsembe yamoto ya kwa Yehova; yotengako ku nsembe yoyamika; mafuta ake, mchira wamafuta wonse, atauchotsa kufupi ku fupa la msana; naichotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo, ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pomwepo, okhala m'chuuno, ndi chokuta cha mphafa chofikira kuimpso. Ndipo wansembe azitenthe pa guwa la nsembe; ndicho chakudya cha nsembe yamoto ya kwa Yehova. Ndipo chopereka chake chikakhala mbuzi, azibwera nayo pamaso pa Yehova; naike dzanja lake pamutu pake, naiphe pa khomo la chihema chokomanako; ndipo ana a Aroni awaze mwazi wake pa guwa la nsembe pozungulira. Ndipo abwere nacho chopereka chake chotengako, ndicho nsembe yamoto ya kwa Yehova; achotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo, ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pomwepo, okhala m'chuuno, ndi chokuta cha mphafa chofikira kuimpso. Ndipo wansembe atenthe izi pa guwa la nsembe; ndizo chakudya cha nsembe yamoto ichite fungo lokoma; mafuta onse nga Yehova. Likhale lemba losatha m'mibadwo yanu m'nyumba zanu zonse, musamadya kapena mafuta kapena mwazi. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Munthu akachimwa, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, nakachitapo kanthu; akalakwa wansembe wodzozedwa ndi kupalamulira anthu; pamenepo azibwera nayo kwa Yehova ng'ombe yamphongo, yopanda chilema, chifukwa cha kuchimwa kwake adakuchita, ikhale nsembe yauchimo. Ndipo adze nayo ng'ombeyo ku khomo la chihema chokomanako pamaso pa Yehova; naike dzanja lake pamutu pa ng'ombeyo, naiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova. Ndipo wansembe wodzozedwayo atengeko mwazi wa ng'ombeyo, nabwere nao ku chihema chokomanako; ndipo wansembeyo aviike chala chake m'mwazimo, nawaze mwaziwo kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova chakuno cha nsalu yotchinga, ya malo opatulika. Ndipo wansembeyo atengeko mwazi, nauike pa nyanga za guwa la nsembe la chofukiza cha fungo lokoma, lokhala m'chihema chokomanako pamaso pa Yehova; nathire mwazi wonse wa ng'ombeyo patsinde pa guwa la nsembe yopsereza, lokhala pa khomo la chihema chokomanako. Ndipo achotse mafuta onse a ng'ombe ya nsembe yauchimo, achotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo, ndi impso ziwiri ndi mafuta ali pomwepo, okhala m'chuuno, ndi chokuta cha mphafa chofikira kuimpso, umo azikachotsera pa ng'ombe ya nsembe yoyamika; ndipo wansembe azitenthe pa guwa la nsembe yopsereza. Natulutse chikopa cha ng'ombeyo, ndi nyama yake yonse, pamodzi ndi mutu wake, ndi miyendo yake, ndi matumbo ake, ndi chipwidza chake, inde ng'ombe yonse, kunja kwa chigono, kunka nayo kumalo koyera, kumene atayako mapulusa, naitenthe pankhuni ndi moto; aitenthe potayira mapulusa. Ndipo khamu lonse la Israele likalakwa osati dala, ndipo chikabisika chinthuchi pamaso pa msonkhano, litachita china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, ndi kupalamula; kukadziwika kuchimwa adachimwako, pamenepo msonkhano uzibwera nayo ng'ombe yamphongo, ikhale nsembe yauchimo, ndipo udze nayo ku khomo la chihema chokomanako. Ndipo akulu a khamulo aike manja ao pamutu pa ng'ombeyo, pamaso pa Yehova; naiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova. Ndipo wansembe wodzozedwayo adze nao mwazi wina wa ng'ombeyo ku chihema chokomanako; naviike chala chake m'mwazi wa nsembewo, nauwaze kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova, chakuno cha nsalu yotchinga. Naike mwazi wina pa nyanga za guwa la nsembe, lokhala pamaso pa Yehova, lokhala m'chihema chokomanako; nathire mwazi wonse patsinde pa guwa la nsembe yopsereza, lokhala pa khomo la chihema chokomanako. Ndipo achotse mafuta ake onse, nawatenthe pa guwa la nsembe. Atero nayo ng'ombeyo; monga umo anachitira ng'ombe ya nsembe yauchimo; ndipo wansembe awachitire chowatetezera, ndipo adzakhululukidwa. Ndipo atulutse ng'ombeyo kunja kwa chigono, ndi kuitentha monga anatenthera ng'ombe yoyamba ija; ndiyo nsembe yauchimo ya kwa msonkhano. Akachimwa mkulu, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova Mulungu wake, napalamula; akamdziwitsa kuchimwa kwake adachimwako, azidza nacho chopereka chake, ndicho tonde wopanda chilema; naike dzanja lake pamutu pa mbuziyo, naiphe pamalo pophera nsembe yopsereza pamaso pa Yehova; ndiyo nsembe yauchimo. Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yauchimo ndi chala chake, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wake patsinde pa guwa la nsembe yopsereza. Ndipo atenthe mafuta ake onse pa guwa la nsembe, monga mafuta a nsembe yoyamika; ndipo wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhululukidwa. Ndipo akachimwa wina wa anthu a m'dziko, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, napalamula; akamdziwitsa kuchimwa kwake adachimwako, azidza nacho chopereka chake mbuzi yaikazi, yopanda chilema, chifukwa cha kuchimwa kwake adakuchita. Aike dzanja lake pamutu pa nsembe yauchimo, naiphe nsembe yauchimo pamalo pa nsembe yopsereza. Ndipo wansembe atengeko mwazi ndi chala chake, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wake wonse patsinde pa guwa la nsembe. Nachotse mafuta ake onse, monga umo amachotsera mafuta pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo awatenthe pa guwa la nsembe akhale fungo lokoma la kwa Yehova; ndi wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhululukidwa. Ndipo akadza nayo nkhosa, ndiyo chopereka chake, ikhale nsembe yauchimo, azidza nayo yaikazi, yopanda chilema. Naike dzanja lake pa mutu wa nsembe yauchimo, ndi kuipha ikhale nsembe yauchimo pamalo pophera nsembe yopsereza. Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yauchimo ndi chala chake, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wake wonse patsinde pa guwa la nsembe; nawachotse mafuta ake onse, monga umo amachotsera mafuta a nkhosa pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo atenthe awa pa guwa la nsembe, monga umo amachitira nsembe zamoto za Yehova; ndipo wansembeyo amchitire chomtetezera pa kuchimwa kwake adakuchimwira, ndipo adzakhululukidwa. Ndipo akachimwa munthu, wakuti adamva mau akuwalumbiritsa, ndiye mboni, kapena wakuona, kapena wakudziwa, koma osawulula, azisenza mphulupulu yake; kapena munthu akakhudza chilichonse chodetsa kapena mtembo wa nyama yodetsa, kapena mtembo wa choweta chodetsa, kapena mtembo wa chokwawa chodetsa, kungakhale kudambisikira, ali wodetsedwa, ndi wopalamula. Kapena akakhudza chodetsa cha munthu, ndicho chodetsa chilichonse akhala wodetsedwa nacho, ndipo chidambisikira; koma pochizindikira akhala wopalamula: kapena munthu akalumbira ndi milomo yake osalingirira kuchita choipa, kapena kuchita chabwino, chilichonse munthu akalumbira osalingirira, ndipo chidambisikira; koma pochizindikira akhala wopalamula chimodzi cha izi: ndipo kudzali, atapalamula chimodzi cha izi, aziwulula chimene adachimwa nacho; nadze nayo nsembe yopalamula kwa Yehova chifukwa cha kulakwa kwake adachimwira, ndiyo nkhosa yaikazi, kapena mbuzi yaikazi, ikhale nsembe yauchimo; ndipo wansembe amchitire chomtetezera chifukwa cha kuchimwa kwake. Ndipo chuma chake chikapanda kufikira nkhosa, wochimwayo adze nayo kwa Yehova nsembe yake yopalamula, njiwa ziwiri, kapena maunda awiri; imodzi ikhale ya nsembe yauchimo, ndi ina ya nsembe yopsereza. Ndipo adze nazo kwa wansembe, ndiye ayambe kubwera nayo ija ya kwa nsembe yauchimo, napotole mutu wake pakhosi pake, osauchotsa; nawazeko mwazi wa nsembe yauchimo pa mbali ya guwa la nsembe; ndi mwazi wotsalira aukamulire patsinde pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yauchimo. Ndipo aikonze inzake ikhale nsembe yopsereza, monga mwa lemba lake; ndipo wansembe amchitire chomtetezera chifukwa cha kuchimwa adachimwira, ndipo adzakhululukidwa. Koma chuma chake chikapanda kufikira njiwa ziwiri kapena maunda awiri, wochimwayo azidza nacho chopereka chake limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, likhale la nsembe yauchimo; asamaikapo mafuta, kapena kuikapo lubani ai; pakuti ndicho nsembe yauchimo. Ndipo adze nacho kwa wansembe, ndi wansembeyo atengeko wodzala manja ukhale chikumbutso chake, nachitenthe pa guwa la nsembe monga umo amachitira nsembe zamoto za Yehova; ndiyo nsembe yauchimo. Ndipo wansembe amchitire chomtetezera chifukwa cha kuchimwa kwake adachimwira chimodzi cha izi, ndipo adzakhululukidwa; ndipo chotsalira chikhale cha wansembe, monga umo amachitira chopereka chaufacho. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Munthu akachita mosakhulupirika, nakachimwa osati dala, pa zopatulika za Yehova, azidza nayo nsembe yake yopalamula kwa Yehova, ndiyo nkhosa yamphongo yopanda chilema, ya m'gulu lake, monga umayesa mtengo wake potchula masekeli a siliva, kunena sekeli wa malo opatulika, ikhale nsembe yopalamula; ndipo abwezere cholakwira chopatulikacho, naonjezepo limodzi la magawo asanu, napereke kwa wansembe; ndi wansembeyo amchitire chomtetezera ndi nkhosa yamphongo ya nsembe yopalamula; ndipo adzakhululukidwa. Ndipo munthu akachimwa, nakachita china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova; angakhale analibe kudziwa, koma wapalamula, azisenza mphulupulu yake. Nadze nayo kwa wansembe nkhosa yamphongo yopanda chilema ya m'khola lake, monga umayesa mtengo wake, ikhale nsembe yopalamula; ndipo wansembeyo amchitire chomtetezera chifukwa cha kusachimwa dala kwake, osakudziwa; ndipo adzakhululukidwa. Iyo ndiyo nsembe yopalamula; munthuyu anapalamula ndithu pamaso pa Yehova. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Akachimwa munthu nakachita mosakhulupirika pa Yehova nakachita monyenga ndi mnansi wake kunena za choikiza, kapena chikole, kapena chifwamba, kapena anasautsa mnansi wake; kapena anapeza chinthu chotayika, nanenapo bodza, nalumbira pabodza; pa chimodzi cha izi zonse amachita munthu, ndi kuchimwapo; pamenepo padzali kuti popeza anachimwa, napalamula, azibweza zofunkha zimene analanda mwachifwamba, kapena chinthuchi adachiona ndi kusautsa mnzake, kapena choikiza anamuikiza, kapena chinthu chotayika anachipeza; kapena chilichonse analumbirapo monama; achibwezere chonsechi, naonjezepo, limodzi la magawo asanu; apereke ichi kwa mwini wake tsiku lotsutsidwa iye. Ndipo adze nayo nsembe yake yopalamula kwa Yehova, ndiyo nkhosa yamphongo yopanda chilema ya m'khola mwake, monga umayesa mtengo wake, ikhale nsembe yopalamula, adze nayo kwa wansembe; ndipo wansembeyo amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova, ndipo adzakhululukidwa; kunena zilizonse akazichita ndi kupalamula nazo. Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, nati, Uza Aroni ndi ana ake, ndi kuti, Chilamulo cha nsembe yopsereza ndi ichi: nsembe yopsereza izikhala pa nkhuni za pa guwa la nsembe usiku wonse kufikira m'mawa; ndipo moto wa pa guwa la nsembe uziyakabe pamenepo. Ndipo wansembe avale mwinjiro wake wabafuta, navale pathupi pake zovala za pamiyendo zabafuta; naole phulusa, moto utanyeketsa nsembe yamoto pa guwa la nsembe, nalitaye m'mphepete mwa guwa la nsembe. Pamenepo avule zovala zake, navale zovala zina, nachotse phulusa kunka nalo kunja kwa chigono, kumalo koyera. Ndipo moto wa pa guwa la nsembe uyakebe pamenepo, wosazima; wansembe ayatsepo nkhuni m'mawa ndi m'mawa; nakonzepo nsembe yopsereza, natenthepo mafuta a nsembe zoyamika. Moto uziyakabe pa guwa la nsembe, wosazima. Ndipo chilamulo cha chopereka chaufa ndicho: ana a Aroni azibwera nacho pamaso pa Yehova ku guwa la nsembe. Ndipo atengeko wodzala manja pa ufa wa chopereka cha ufa wosalala, ndi pa mafuta ake, ndi lubani lonse lili pa chopereka chaufa, nazitenthe pa guwa la nsembe, zichite fungo lokoma, ndizo chikumbutso chake cha kwa Yehova. Ndipo chotsalira chake adye Aroni ndi ana ake; achidye chopanda chotupitsa m'malo opatulika; pa bwalo la chihema chokomanako achidye. Asachiphike ndi chotupitsa. Ndachipereka chikhale gawo lao lochokera pa nsembe zanga zamoto; ndicho chopatulika kwambiri, monga nsembe yauchimo, ndi monga nsembe yopalamula. Amuna onse a mwa ana a Aroni adyeko, ndilo lemba losatha la ku mibadwo yanu, chiwachokere ku nsembe zamoto za Yehova; aliyense wakuzikhudza izi adzakhala wopatulika. Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, nati, Chopereka cha Aroni ndi ana ake, chimene azibwera nacho kwa Yehova tsiku la kudzozedwa iye ndi ichi: limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, likhale chopereka chaufa kosalekeza, nusu lake m'mawa, nusu lake madzulo. Chikonzeke pachiwaya ndi mafuta; udze nacho chokazinga; chopereka chaufa chazidutsu ubwere nacho, chikhale fungo lokoma la kwa Yehova. Ndipo wansembe wodzozedwa m'malo mwake, wa mwa ana ake, achite ichi; likhale lemba losatha; achitenthe konse kwa Yehova. Ndipo zopereka zaufa zonse za wansembe azitenthe konse; asamazidya. Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, nati, Lankhula ndi Aroni ndi ana ake, ndi kuti, Chilamulo cha nsembe yauchimo ndi ichi: Pamalo pophera nsembe yopsereza ndipo pophera nsembe yauchimo pamaso pa Yehova; ndiyo yopatulika kwambiri. Ndipo azidya iyi wansembe amene aipereka chifukwa cha zoipa; aidyere m'malo opatulika, pa bwalo la chihema chokomanako. Aliyense akakhudza nyama yake adzakhala wopatulika; ndipo akawaza mwazi wake wina pa chovala chilichonse, utsuke chimene adauwazacho m'malo opatulika. Ndipo mphika wadothi umene anaphikamo nyamayi auswe, koma ngati anaiphika mu mphika wamkuwa, atsuke uwu, nautsukuluze ndi madzi. Amuna onse a mwa ansembe adyeko; ndiyo yopatulika kwambiri. Koma asadye nsembe yauchimo iliyonse, imene amadza nao mwazi wake ku chihema chokomanako kutetezera nao m'malo opatulika; aitenthe ndi moto. Ndipo chilamulo cha nsembe yopalamula ndi ichi: ndiyo yopatulika kwambiri. Pamalo pophera nsembe yopsereza ndipo aziphera nsembe yopalamula; nawaze mwazi wake pa guwa la nsembe pozungulira. Ndipo achotseko, nabwere nao mafuta ake onse; mchira wamafuta, ndi mafuta akukuta matumbo, ndi impso ziwiri, ndi mafuta a pamenepo, okhala m'chuuno, ndi chokuta cha mphafa chofikira kuimpso; ndipo wansembe atenthe izi pa guwa la nsembe, nsembe yamoto ya kwa Yehova; ndiyo nsembe yopalamula. Amuna onse a mwa ansembe adyeko; adyere m'malo opatulika; ndiyo yopatulika kwambiri. Monga nsembe yauchimo, momwemo nsembe yopalamula; pa zonse ziwirizi pali chilamulo chimodzi; ikhale yake ya wansembeyo, amene achita nayo chotetezera. Ndipo chikopa cha nsembe yopsereza chikhale chakechake cha wansembe, amene anabwera nayo nsembe yopsereza ya munthu aliyense. Ndipo nsembe zaufa zonse zophika mumchembo, ndi zonse zokonzeka mumphika, ndi pachiwaya, zikhale za wansembe amene wabwera nazo. Ndipo nsembe zonse zaufa zosanganiza ndi mafuta, kapena zouma zikhale za ana onse a Aroni, alandireko onse. Ndipo chilamulo cha nsembe zoyamika, zimene azibwera nazo kwa Yehova ndi ichi: akabwera nayo kuti ikhale nsembe yolemekeza, azibwera nato, pamodzi ndi nsembe yolemekeza, timitanda topanda chotupitsa tosanganiza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda chotupitsa todzoza ndi mafuta, ndi timitanda tootcha, ta ufa wosalala tosanganiza ndi mafuta. Abwere nacho chopereka chake pamodzi ndi timitanda ta mkate wachotupitsa, pamodzi ndi nsembe yolemekeza, ya nsembe zoyamika zake. Ndipo pa zopereka zonsezi atengepo ndi kubwera nako kamtanda kamodzi, kuti kakhale ka nsembe yokweza ya kwa Yehova; kakhale ka wansembe wakuwaza mwazi wa nsembe zoyamika. Kunena za nyama ya nsembe yolemekeza ya nsembe zoyamika zake, aziidya tsiku lomwelo lakuipereka; asasiyeko kufikira m'mawa. Koma nsembe ya chopereka chake ikakhala ya chowinda, kapena chopereka chaufulu, aidye tsiku lomwelo anabwera nayo nsembe yake; ndipo m'mawa adye chotsalirapo; koma chotsalira pa nyama ya nsembeyo tsiku lachitatu, achitenthe. Ndipo akadyako nyama ya nsembe zoyamika zake tsiku lachitatu, sikuvomerezeka kumene; sadzamwerengera wobwera nayo; ndiyo chinthu chonyansa, ndipo munthu wakudyako adzasenza mphulupulu zake. Ndipo nyama yokhudza kanthu kalikonse kodetsa isadyeke; aitenthe ndi moto. Koma za nyama ina, aliyense ayera aidyeko. Koma munthu akadya nyama ya nsembe zoyamika za Yehova, pokhala nacho chomdetsa, munthuyo asadzidwe kwa anthu a mtundu wake. Ndipo munthu akakhudza chinthu chodetsa, chodetsa cha munthu, kapena chodetsa cha zoweta, kapena chilichonse chonyansa chodetsa, nakadyako nyama ya nsembe zoyamika za Yehova, munthuyo asadzidwe kwa anthu a mtundu wake. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Lankhula ndi ana a Israele ndi kuti, Musamadya mafuta ali onse, a ng'ombe, kapena a nkhosa, kapena a mbuzi. Ndipo mafuta a iyo idafa yokha, ndi mafuta a iyo idajiwa ndi chilombo ayenera ntchito iliyonse, koma musamadya awa konsekonse. Pakuti aliyense akadya mafuta a nyama imene amabwera nayo ikhale nsembe yamoto ya kwa Yehova, munthu amene akadya awa asadzidwe kwa anthu a mtundu wake. Ndipo musamadya mwazi uliwonse, kapena wa mbalame, kapena wa nyama, m'nyumba zanu zonse. Aliyense akadya mwazi uliwonse, munthuyo asadzidwe kwa anthu a mtundu wake. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Wakubwera nayo nsembe yoyamika yake kwa Yehova, azidza nacho chopereka chake kwa Yehova chochokera ku nsembe yoyamika yake; adze nazo m'manja mwake nsembe zamoto za Yehova; adze nao mafuta pamodzi ndi nganga, kuti aweyule ngangayo ikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova. Ndipo wansembeyo atenthe mafutawo pa guwa la nsembe; koma ngangayo ikhale ya Aroni ndi ana ake. Ndipo mwendo wathako wa ku dzanja lamanja muupereke kwa wansembe ukhale nsembe yokweza yochokera ku nsembe zoyamika zanu. Mwendo wathako wa ku dzanja lamanja ukhale gawo lake la iyeyu mwa ana a Aroni wakubwera nao mwazi wa zopereka zoyamika, ndi mafuta. Pakuti ndatengako kwa ana a Israele, ku nsembe zoyamika zao, nganga ya nsembe yoweyula, ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja wa nsembe yokweza; ndipo ndazipereka kwa Aroni wansembe ndi kwa ana ake, zikhale zoyenera iwo kosatha zochokera kwa ana a Israele. Ili ndi gawo la Aroni, ndi gawo la ana ake, lochokera ku nsembe zamoto za Yehova, analinena, tsiku limene Iye anawasendeza alowe utumiki wa ansembe a Yehova; limene Yehova anauza ana a Israele aziwapatsa, tsiku limene Iye anawadzoza. Likhale lemba losatha mwa mibadwo yao. Icho ndi chilamulo cha nsembe yopsereza, cha nsembe yaufa, cha nsembe yauchimo, ndi cha nsembe yopalamula, ndi cha kudzaza dzanja, ndi cha nsembe zoyamika; chimene Yehova analamulira Mose m'phiri la Sinai, tsikuli anauza ana a Israele abwere nazo zopereka zao kwa Yehova, m'chipululu cha Sinai. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Tenga Aroni ndi ana ake pamodzi naye ndi zovalazo, ndi mafuta odzozawo; ndi ng'ombe ya nsembe yauchimoyo, ndi nkhosa zamphongo ziwirizo, ndi dengu la mkate wopanda chotupitsawo; nusonkhanitse khamu lonse ku khomo la chihema chokomanako. Ndipo Mose anachita monga Yehova anamuuza; ndi khamulo linasonkhana pa khomo la chihema chokomanako. Ndipo Mose anati kwa msonkhanowo, Ichi ndi chimene Yehova adauza kuti chichitike. Ndipo Mose anabwera nao Aroni ndi ana ake, nawasambitsa ndi madzi. Ndipo anamveka ndi malaya a m'kati, nammanga m'chuuno ndi mpango, namveka ndi mwinjiro, namveka ndi efodi, nammanga m'chuuno ndi mpango wa efodi nammanga nao pathupi pake. Ndipo anamuika chapachifuwa; naika m'chapachifuwa Urimu ndi Tumimu. Naika nduwirayo pamutu pake; ndi panduwira, pamphumi pake anaika golide waphanthiphanthi, ndiwo korona wopatulika; monga Yehova adauza Mose. Ndipo Mose anatenga mafuta odzoza, nadzoza Kachisi, ndi zonse zili m'mwemo, nazipatula. Ndipo anawazako pa guwa la nsembe kasanu ndi kawiri, nadzoza guwa la nsembe, ndi zipangizo zake zonse, ndi mkhate ndi tsinde lake, kuzipatula. Ndipo anatsanulirako mafuta odzoza pamutu pa Aroni, namdzoza kumpatula. Ndipo Mose anatenga ana a Aroni, nawaveka malaya a m'kati, nawamanga m'chuuno ndi mipango, nawamanga akapa; monga Yehova adzauza Mose. Ndipo anabwera nayo ng'ombe ya nsembe yauchimo; ndipo Aroni ndi ana ake amuna anaika manja ao pa mutu wa ng'ombe ya nsembe yauchimo. Ndipo anaipha; ndi Mose anatenga mwaziwo, naupaka ndi chala chake pa nyanga za guwa la nsembe pozungulira; nayeretsa guwa la nsembe, nathira mwazi patsinde pa guwa la nsembe, nalipatula, kuti alichitire cholitetezera. Ndipo anatenga mafuta onse a pamatumbo, ndi chokuta cha mphafa, ndi impso ziwiri, ndi mafuta ake, ndipo Mose anazitentha pa guwa la nsembe. Koma ng'ombeyo, ndi chikopa chake, ndi nyama yake, ndi chipwidza chake, anazitentha ndi moto kunja kwa chigono; monga Yehova adamuuza Mose. Ndipo anabwera nayo nkhosa yamphongo ya nsembe yopsereza; ndipo Aroni ndi ana ake amuna anaika manja ao pamutu pa mphongoyo. Ndipo anaipha; ndi Mose anawaza mwazi wake pa guwa la nsembe pozungulira. Ndipo anapadzula mphongoyo ziwalo zake; ndi Mose anatentha mutuwo ndi ziwalo, ndi mafuta. Koma anatsuka matumbo ndi miyendo ndi madzi; ndi Mose anatentha mphongo yonse pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza yochita fungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose. Ndipo anabwera nayo nkhosa yamphongo yinayo, ndiyo mphongo ya kudzaza manja; ndipo Aroni ndi ana ake amuna anaika manja ao pa mutu wa mphongoyo. Ndipo anaipha; ndi Mose anatengako mwazi wake naupaka pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la Aroni, ndi pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja lake, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja. Pamenepo anabwera nao ana amuna a Aroni, ndi Mose anatengako mwazi, naupaka pa ndewerere ya khutu lao la ku dzanja lamanja, ndi pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja lao, ndi pa chala chachikulu cha phazi lao la ku dzanja lamanja; ndipo Mose anawaza mwaziwo pa guwa la nsembe pozungulira. Ndipo anatenga mafutawo ndi mchira wamafuta, ndi mafuta onse a pamatumbo, ndi chokuta cha mphafa, ndi impso ziwiri, ndi mafuta ake, ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja; ndipo mu dengu la mkate wopanda chotupitsa wokhala pamaso pa Yehova, anatengeramo kamtanda kamodzi kopanda chotupitsa, ndi kamtanda kamodzi ka mkate wamafuta, ndi kamtanda kamodzi kaphanthi, natiika pa mafutawo, ndi pa mwendo wathako wa ku dzanja lamanja; anaika zonsezi m'manja mwa Aroni, ndi m'manja mwa ana ake amuna, naziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova. Pamenepo Mose anazichotsa ku manja ao, nazitentha pa guwa la nsembe, pa nsembe yopsereza; ndizo nsembe zodzaza manja zochita fungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova. Ndipo Mose anatenga ngangayo naiweyula, nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndilo gawo la Mose la ku nkhosa yamphongo ya kudzaza manja; monga Yehova adamuuza Mose. Ndipo Mose anatengako mafuta odzoza, ndi mwazi unakhala pa guwa la nsembewo, naziwaza pa Aroni, pa zovala zake, ndi pa ana ake amuna, ndi pa zovala za ana ake amuna omwe; napatula Aroni, ndi zovala zake, ndi ana ake amuna, ndi zovala za ana ake amuna omwe. Ndipo Mose anati kwa Aroni ndi kwa ana ake amuna, Phikani nyamayi pakhomo pa chihema chokomanako; ndipo muidyere komweko ndi mkate uli mu dengu la nsembe zodzaza manja, monga ndinauza, ndi kuti, Aroni ndi ana ake aidye. Koma chotsalira cha nyama ndi mkate muchitenthe ndi moto. Ndipo musatuluka pa khomo la chihema chokomanako masiku asanu ndi awiri, kufikira anakwanira masiku a kudzaza manja kwanu; pakuti adzaze manja anu masiku asanu ndi awiri. Monga anachita lero lino, momwemo Yehova anauza kuchita, kukuchitirani chotetezera. Ndipo mukhale pakhomo pa chihema chokomanako masiku asanu ndi awiri, usana ndi usiku, ndi kusunga chilangizo cha Yehova, kuti mungafe; pakuti anandiuza kotero. Ndipo Aroni ndi ana ake amuna anachita zonse zimene Yehova anauza pa dzanja la Mose. Ndipo kunali, tsiku lachisanu ndi chitatu, kuti Mose anaitana Aroni ndi ana ake amuna, ndi akulu a Israele; ndipo anati kwa Aroni, Dzitengere mwanawang'ombe wamwamuna, akhale nsembe yauchimo, ndi nkhosa yamphongo ikhale nsembe yopsereza, zopanda chilema, nubwere nazo pamaso pa Yehova. Nunene kwa ana a Israele, ndi kuti, Dzitengereni tonde akhale nsembe yauchimo; ndi mwanawang'ombe, ndi mwanawankhosa, a chaka chimodzi, opanda chilema, akhale nsembe yopsereza; ndi ng'ombe, ndi nkhosa yamphongo zikhale zakuyamika, kuziphera nsembe pamaso pa Yehova; ndi nsembe yaufa yosanganiza ndi mafuta; pakuti lero Yehova wakuonekerani inu. Pamenepo anatenga zimene Mose anawauza, napita nazo pakhomo pa chihema chokomanako; ndi msonkhano wonse unasendera kufupi nuimirira pamaso pa Yehova. Ndipo Mose anati, Ichi ndi chimene Yehova anakuuzani kuti muchichite; ndipo ulemerero wa Yehova udzaonekera kwa inu. Ndipo Mose anati kwa Aroni, Sendera kufupi kwa guwa la nsembe, nukonze nsembe yako yauchimo, ndi nsembe yako yopsereza, nudzichitire wekha ndi anthuwo chotetezera; nupereke chopereka cha anthu, ndi kuwachitira chotetezera; monga Yehova anauza. Pamenepo Aroni anasendera kufupi kwa guwa la nsembe, napha mwanawang'ombe wa nsembe yauchimo, ndiyo ya kwa iye yekha. Ndipo ana a Aroni anasendera nao mwazi kwa iye; ndipo anaviika chala chake m'mwazimo naupaka pa nyanga za guwa la nsembe, nathira mwaziwo patsinde pa guwa la nsembe; koma mafutawo, ndi impso, ndi chokuta cha mphafa za nsembe yauchimo, anazitentha pa guwa la nsembe; monga Yehova anauza Mose. Ndipo anatentha ndi moto nyamayi ndi chikopa kunja kwa chigono. Ndipo anapha nsembe yopsereza; ndi ana a Aroni anapereka mwaziwo kwa iye, ndipo anauwaza pa guwa la nsembe pozungulira. Ndipo anapereka nsembe yopsereza kwa iye, chiwalochiwalo, ndi mutu wake; ndipo anazitentha pa guwa la nsembe. Ndipo anatsuka matumbo ndi miyendo, nazitentha pa nsembe yopsereza pa guwa la nsembe. Ndipo anabwera nacho chopereka cha anthu, natenga mbuzi ya nsembe yauchimo ndiyo ya kwa anthu, naipha, naipereka nsembe yauchimo, monga yoyamba ija. Ndipo anabwera nayo nsembe yopsereza naipereka monga mwa lemba lake. Ndipo anabwera nayo nsembe yaufa, natengako wodzala dzanja, nautentha pa guwa la nsembe, angakhale adatentha nsembe yopsereza ya m'mawa. Anaphanso ng'ombe, ndi nkhosa yamphongoyo, ndizo nsembe zoyamika za anthu; ndi ana a Aroni anapereka kwa iye mwaziwo, ndipo anauwaza pa guwa la nsembe pozungulira, ndi mafuta a ng'ombe; ndi a nkhosa yamphongoyo, ndi mchira wamafuta, ndi chophimba matumbo, ndi impso, ndi chokuta cha mphafa; ndipo anaika mafuta pa ngangazo, natentha mafutawo pa guwa la nsembe. Ndipo Aroni anaweyula ngangazo ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja zikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; monga Iye anauza Mose. Ndipo Aroni anakweza dzanja lake kulozera anthu, nawadalitsa; natsika kuja anapereka nsembe yauchimo, ndi nsembe yopsereza, ndi nsembe zoyamika. Ndipo Mose ndi Aroni analowa ku chihema chokomanako, natuluka, nadalitsa anthu; ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera kwa anthu onse. Ndipo unatuluka moto pamaso ya Yehova, nunyeketsa nsembe yopsereza ndi mafuta pa guwa la nsembe; ndipo pakuchiona anthu onse anafuula, nagwa nkhope zao pansi. Ndipo ana a Aroni, Nadabu ndi Abihu anatenga yense mbale yake ya zofukiza, naikamo moto, naikapo chofukiza, nabwera nao pamaso pa Yehova moto wachilendo, umene sanawauze. Ndipo panatuluka moto pamaso pa Yehova, nuwatha, nafa iwo pamaso ya Yehova. Ndipo Mose anati kwa Aroni, Ichi ndi chimene Yehova ananena, ndi kuti, Mwa iwo akundiyandikiza ndipatulidwa Ine, ndi pamaso pa anthu onse ndilemekezedwa. Ndipo Aroni anakhala chete. Ndipo Mose anaitana Misaele ndi Elizafani, ana a Uziyele, mbale wa atate wa Aroni, nanena nao, Senderani pafupi, nyamulani abale anu muwachotse pakhomo pa malo opatulika kunka nao kunja kwa chigono. Pamenepo anasendera pafupi, nawanyamula osawavula malaya ao a m'kati, kunka nao kunja kwa chigono, monga Mose adauza. Ndipo Mose anati kwa Aroni, ndi kwa Eleazara ndi Itamara ana ake, Musawinda tsitsi, musang'amba zovala zanu; kuti mungafe, ndi kuti angakwiye Iye ndi khamu lonse; koma abale anu, mbumba yonse ya Israele, alire chifukwa cha motowu Yehova anauyatsa. Ndipo musatuluka pakhomo pa chihema chokomanako, kuti mungafe, pakuti mafuta odzoza a Yehova ali pa inu. Ndipo anachita monga mwa mau a Mose. Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, nati, Usamamwa vinyo, kapena choledzeretsa, iwe ndi ana ako omwe, m'mene mulowa m'chihema chokomanako, kuti mungafe; likhale lemba losatha mwa mibadwo yanu; ndi kuti musiyanitse pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba, ndi pakati pa zodetsedwa ndi zoyera; ndi kuti muphunzitse ana a Israele malemba onse amene Yehova analankhula nao ndi dzanja la Mose. Ndipo Mose ananena ndi Aroni, ndi Eleazara ndi Itamara, ana ake otsala, Tengani nsembe yaufa yotsalira ku nsembe zamoto za Yehova, ndi kuidya yopanda chotupitsa pafupi pa guwa la nsembe; pakuti ndiyo yopatulika kwambiri; ndipo muziidyera kumalo kopatulika, popeza ndiyo gawo lako, ndi gawo la ana ako, lochokera ku nsembe zamoto za Yehova; pakuti anandiuza chotero. Ndi nganga yoweyula ndi mwendo wokweza mudyere izi pamalo poyera; iwe ndi ana ako amuna, ndi ana ako akazi omwe, popeza zapatsidwa gawo lako ndi gawo la ana ako amuna, zochokera ku nsembe zoyamika za ana a Israele. Mwendo wokweza, ndi nganga yoweyula adze nao pamodzi ndi nsembe zamoto zamafuta, aziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndipo zikhale zako ndi za ana ako amuna, mwa lemba losatha; monga Yehova anauza. Ndipo Mose anafunafuna mbuzi ya nsembe yauchimo, ndipo taonani, adaitentha. Ndipo anapsa mtima pa Eleazara ndi Itamara, ana otsalawo a Aroni, nati, Mwalekeranji kudya nsembe yauchimo m'malo opatulika, pakuti ndiyo yopatulika kwambiri, ndipo Iye anakupatsani iyo, kuchotsera nayo mphulupulu ya khamulo, kuwachitira chowatetezera pamaso pa Yehova? Taonani, sanalowe nao mwazi wake m'malo opatulika m'katimo; mukadaidyera ndithu m'malo opatulika, monga ndinakuuzani. Ndipo Aroni analankhula ndi Mose, nati, Taonani, lero abwera nayo nsembe yao yauchimo ndi nsembe yao yopsereza pamaso pa Yehova; ndipo zandigwera zotere; ndikadadya nsembe yauchimo lero, kukadakomera kodi pamaso pa Yehova? Pamene Mose adamva ichi chidamkomera pamaso pake. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati nao, Nenani ndi ana a Israele, ndi kuti, Izi ndi zamoyo zimene muyenera kumadya mwa nyama zonse zili pa dziko lapansi. Nyama iliyonse yogawanika chiboda, nikhala yogawanikadi chiboda, ndi yobzikula, imeneyo muyenera kudya. Koma izi zokha simuyenera kuzidya mwa zobzikulazo, kapena zogawanika chiboda; ngamira, angakhale abzikula, koma yosagawanika chiboda, muziiyesa yodetsedwa. Ndi mbira, ingakhale ibzikula koma yosagawanika chiboda, muiyese yodetsedwa. Ndi kalulu, popeza abzikula koma wosagawanika chiboda, mumuyese wodetsedwa. Ndi nkhumba, popeza igawanika chiboda, nikhala yogawanikadi chiboda, koma yosabzikula, muiyese yodetsedwa. Nyama yake musamaidya, mitembo yake musamaikhudza; muziyese zodetsedwa. Mwa zonse zili m'madzi muyenera kumadya izi: zilizonse zili nazo zipsepse ndi mamba m'madzi, m'nyanja, ndi m'mitsinje, zimenezo muyenera kumadya. Koma zilizonse zilibe zipsepse ndi mamba m'nyanja, ndi m'mitsinje, mwa zonse zokwawa za m'madzi, ndi mwa zamoyo zonse zili m'madzi, muziziyesa zonyansa; inde muziyese zonyansa; musamadya nyama zao; mitembo yao zikunyansireni. Zilizonse zopanda zipsepse kapena mamba m'madzimo muziyese zonyansa. Ndipo mwa mbalame muziziyesa zonyansa izi; siziyenera kuzidya, zonyansa ndi izi: mphungu, ndi nkhwazi, ndi chikambi; ndi muimba, ndi mphamba mwa mtundu wake; khungubwi mwa mtundu wake; ndi nthiwatiwa, ndi chipudo, ndi kakowa, ndi kabawi mwa mtundu wake; ndi nkhutukutu ndi nswankhono ndi manchichi; tsekwe, vuwo, ndi dembo; indwa, ndi chimeza monga mwa mtundu wake, ndi sadzu, ndi mleme. Zokwawa zonse zakuuluka zokhala ndi miyendo inai, muziyesa izi zonyansa. Koma muyenera kudya izi mwa zokwawa zonse zakuuluka, zokhala ndi miyendo inai, zokhala ndi miyendo pa mapazi ao, ya kuthumpha nayo pansi; mwa zimenezi muyenera kudya izi: dzombe mwa mtundu wake, ndi chirimamine mwa mitundu yake, ndi njenjete mwa mtundu wake ndi tsokonombwe mwa mitundu yake. Koma zokwawa zonse zakuuluka, za miyendo inai, muziyese zonyansa. Ndipo izi zikudetsani: aliyense akhudza mtembo wake adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; ndipo aliyense akanyamulako nyama ya mtembo wake azitsuka zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo. Nyama iliyonse yakugawanika chiboda, koma yosagawanikitsa, ndi yosabzikula, muiyese yodetsa; aliyense wakuikhudza adzakhala wodetsedwa. Ndipo iliyonse iyenda yopanda chiboda mwa zamoyo zonse za miyendo inai, muiyese yodetsedwa; aliyense wokhudza mtembo wake adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo. Ndipo iye amene akanyamula mtembo wake atsuke zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; muziyese izi zodetsa. Ndipo izi ndi zimene muziziyesa zodetsedwa mwa zinthu zokwawa zakukwawa pansi; likongwe, ndi mbewa, ndi msambulu mwa mtundu wake; ndi gondwa, ndi mng'azi, ndi buluzi, ndi dududu, ndi birimankhwe. Izi ndi zimene muziyese zodetsa, mwa zonse zakukwawa; aliyense azikhudza zitafa, adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo. Ndipo chilichonse chakufa cha izi chikagwera kanthu, kanthuka kadzakhala kodetsedwa; ngakhale chipangizo chamtengo, kapena chovala, kapena chikopa kapena thumba, chipangizo chilichonse chimene agwira nacho ntchito, achiviike m'madzi, ndipo chidzakhala chodetsedwa kufikira madzulo; pamenepo chidzakhala choyera. Ndipo chilichonse cha izi chikagwa m'chotengera chilichonse chadothi, chinthu chokhala m'mwemo chidetsedwa, ndi chotengeracho muchiswe. Chakudya chilichonse chokhala m'mwemo, chokonzeka ndi madzi, chidzakhala chodetsedwa; ndi chakumwa chilichonse m'chotengera chotere chidzakhala chodetsedwa. Ndipo kanthu ka mtembo wake kakagwa pa zinthu zilizonse zidzakhala zodetsedwa; ngakhale mchembo kapena mphika wovundikika, aziswe; zodetsa izi, muziyese zodetsedwa. Koma kasupe kapena chitsime muli madzi, zidzakhala zoyera; koma iye amene akhudza mitembo yao adzadetsedwa. Ndipo kanthu ka mtembo wake kakagwa pa mbeu yofesa, ikati ifesedwe, idzakhala yoyera. Koma akathira madzi pa mbeuyi, ndi kanthu ka mtembo wake kakagwapo, muiyese yodetsedwa. Ndipo ikafa nyama yakudya, iye amene akhudza mtembo wake adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo. Ndipo iye wakudya kanthu ka mtembo wake azitsuka zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; iyenso wakunyamula mtembo wake atsuke zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo. Ndipo zokwawa zonse zakukwawa pa dziko lapansi zikhale zonyansa; musamazidya. Zonse zoyenda chafufumimba, ndi zonse za miyendo inai, kapena zonse zokhala nayo miyendo yambiri ndi zokwawa zonse zakukwawa pansi, musamazidya; popeza ndizo zonyansa. Musamadzinyansitsa ndi chokwawa chilichonse chakukwawa, musamadzidetsa nazo, kuti mukadziipse nazo. Pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu; potero dzipatuleni, ndipo muzikhala oyera; pakuti Ine ndine woyera; ndipo musamadziipsa ndi chokwawa chilichonse chakukwawa pansi. Pakuti Ine ndine Yehova amene ndinakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito, ndikhale Mulungu wanu; chifukwa chake mukhale oyera, popeza Ine ndine woyera. Ichi ndi chilamulo cha nyama, ndi cha mbalame, ndi cha zamoyo zonse zakuyenda m'madzi, ndi cha zamoyo zonse zakukwawa pansi; kusiyanitsa pakati zodetsa ndi zoyera, ndi pakati pa zamoyo zakudya ndi zamoyo zosadya. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Nena ndi ana a Israele, ndi kuti, Akaima mkazi, nakabala mwana wamwamuna, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri; monga masiku ake akukhala padera, podwala iye, adzakhala wodetsedwa. Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu adule khungu la mwanayo. Ndipo akhale m'mwazi wa kumyeretsa kwake masiku makumi atatu kudza atatu; asakhudze kanthu kopatulika, kapena kulowa m'malo opatulika, kufikira adakwanira masiku a kumyeretsa kwake. Koma akabala mwana wamkazi, akhale wodetsedwa masabata awiri, monga umo amakhala padera; ndipo adzakhala m'mwazi wa kumyeretsa kwake masiku makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi limodzi. Ndipo atakwanira masiku a kumyeretsa kwake pa mwana wamwamuna, kapena mwana wamkazi, adze naye mwanawankhosa wa chaka chimodzi ikhale nsembe yopsereza, ndi bunda, kapena njiwa zikhale nsembe yauchimo, ku khomo la chihema chokomanako, kwa wansembe; ndipo iye abwere nayo pamaso pa Yehova, namchitire chomtetezera mkaziyo, ndipo adzakhala woyeretsedwa wochira kukha mwazi kwake. Ichi ndi chilamulo cha kwa iye wakubala, kapena mwana wamwamuna kapena wamkazi. Ndipo chuma chake chikapanda kufikira nkhosa, atenge njiwa ziwiri kapena maunda awiri; lina likhale nsembe yopsereza, ndi lina nsembe yauchimo; ndi wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhala woyera. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati, Ngati munthu ali nacho chotupa, kapena nkhanambo, kapena chikanga pa khungu la thupi lake, ndipo isandulika nthenda yakhate pa khungu la thupi lake, azifika kwa Aroni wansembe, kapena kwa mmodzi wa ana ake ansembe; ndipo wansembe aione nthenda pa khungu la thupi; ndipo ngati tsitsi la panthenda lasanduka la mbu, ndi nthenda ikaoneka yapitirira khungu la thupi lake, ndiyo nthenda yakhate; ndipo wansembe amuone, namutche wodetsedwa. Koma ngati chikanga chikhala chotuwa pa khungu la thupi lake, ndipo chikaoneka chosapitirira khungu, ndi tsitsi lake losasanduka loyera, pamenepo wansembe ambindikiritse wanthendayo masiku asanu ndi awiri; ndipo wansembe amuonenso tsiku lachisanu ndi chiwiri; ndipo taonani, monga momwe apenyera iye, nthenda yaima, nthenda siinapitirira pakhungu, pamenepo wansembe ambindikiritsenso masiku asanu ndi awiri ena; ndipo wansembe amuonenso tsiku lachisanu ndi chiwiri, ndipo taonani, nthenda yazimba yosapitirira khungu nthendayi, pamenepo wansembe amutche iye woyera, ndiyo nkhanambo chabe; ndipo atsuke zovala zake, ndiye woyera; koma nkhanambo ikapitirira khungu, atadzionetsa kwa wansembe kuti atchedwe woyera, adzionetsenso kwa wansembe; ndipo wansembe aone, ndipo taonani, ngati nkhanambo yapitirira khungu, wansembe amutche wodetsedwa, ndilo khate. Pamene nthenda yakhate ili mwa munthu, azimfikitsa kwa wansembe; ndipo wansembe aone, ndipo taonani, ngati pali chotupa choyera pakhungu, ndipo chasanduliza tsitsi likhale loyera, ndipo pachotupa pali mnofu wofiira, ndilo khate lakale pa khungu la thupi lake, ndipo wansembe amutche wodetsedwa; asambindikiretse popeza ali wodetsedwa. Ndipo ngati khate libukabuka pakhungu, ndi khate lakuta khungu lonse la wanthendayo kuyambira mutu wake kufikira mapazi ake, monga momwe apenyera wansembe; pamenepo wansembe aone, ndipo taonani, ngati khate lakuta thupi lake, amutche woyera wanthendayo; patuwa ponsepo; ndiye woyera. Koma tsiku lililonse ukaoneka pa iye mnofu wofiira, adzakhala wodetsedwa. Ndipo wansembe aone mnofu wofiirawo, namutche wodetsedwa; mnofu wofiira ndiwo wodetsa; ndilo khate. Kapena mnofu wofiira ukasandukanso, nusandulika wotuwa, afike kwa wansembe, ndi wansembe amuone, ndipo taonani, ngati nthenda yasandulika yotuwa, wansembe amutche woyera wanthendayo; ndiye woyera. Ndipo pamene thupi lili ndi chilonda pakhungu pake, ndipo chapola, ndipo padali chilonda pali chotupa choyera, kapena chikanga chotuuluka, pamenepo achionetse kwa wansembe; ndipo wansembe aone, ndipo taonani, ngati chioneka chakumba kubzola khungu, ndipo tsitsi lake lisanduka lotuwa, pamenepo wansembe amutche wodetsedwa; ndiyo nthenda yakhate yabuka m'chilondamo. Koma wansembe akachiona, ndipo taonani, palibe tsitsi loyera pamenepo, ndipo sichinakumba kubzola khungu, koma chazimba, pamenepo wansembe ambindikiritse masiku asanu ndi awiri; ndipo ngati chapitirira khungu, wansembe amutche wodetsedwa; ndilo khate. Koma ngati chikanga chaima pomwepo, chosakula, ndicho chipsera cha chilonda; ndipo wansembe amutche woyera. Kapena pamene thupi lidapsa ndi moto pakhungu pake, ndipo mnofu wofiira wakupsawo usanduka chikanga chotuuluka, kapena chotuwa; pamenepo wansembe achione; ndipo taonani, ngati tsitsi la chikanga lasanduka lotuwa, ndipo chioneka chakumba kubzola khungu; pamenepo ndilo khate lobuka m'kupsamo; ndipo wansembe azimutcha wodetsedwa ndi nthenda yakhate. Koma akaonapo wansembe, ndipo taonani, mulibe tsitsi loyera m'chikangamo, ndipo sichikumba kubzola khungu, koma chazimba; pamenepo wansembe ambindikiritse masiku asanu ndi awiri; ndipo wansembe amuone tsiku lachisanu ndi chiwiri; ngati chakula pakhungu, wansembe amutche wodetsedwa; ndiyo nthenda yakhate. Ndipo ngati chikanga chiima pomwepo, chosakula pakhungu koma chazimba; ndicho chotupa chakupsa; ndipo wansembe amutche woyera; pakuti ndicho chipsera chakupsa. Ndipo ngati mwamuna kapena mkazi ali ndi nthenda pamutu kapena pandevu, wansembe aziona nthenda; ndipo taonani, ngati ioneka yokumba kubzola khungu, ndipo pali tsitsi loyezuka lotetemera; pamenepo wansembe amutche wodetsedwa; ndiyo mfundu, ndilo khate la mutu kapena ndevu. Ndipo wansembe akaona nthenda yamfundu, ndipo taonani, ioneka yosakumba kubzola khungu, ndipo palibe tsitsi lakuda pamenepo, wansembe ambindikiritse iye ali ndi mfundu masiku asanu ndi awiri; ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembe aone nthendayi; ndipo taonani, ngati mfundu njosakula, ndipo mulibe tsitsi loyezuka, ndipo mfundu ikaoneka yosakumba kubzola khungu, pamenepo azimeta, koma osameta pamfundu; ndipo wansembe ambindikiritse iye wamfundu masiku asanu ndi awiri ena; ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri aone mfunduyo; ndipo taonani, ngati mfundu njosakula pakhungu, ndipo ioneka yosakula kubzola khungu, wansembe amutche woyera, ndipo iye atsuke zovala zake, nakhala woyera. Koma ngati mfundu ikula pakhungu atatchedwa woyera; pamenepo wansembe amuone, ndipo taonani, ngati mfundu yakula pakhungu, wansembe asafunefune tsitsi loyezuka, ndiye wodetsedwa. Koma monga momwe apenyera iye, ngati mfundu yaima pomwe, ndipo pamera tsitsi lakuda, mfundu yapola, ndiye woyera, ndipo wansembe amutche woyera. Ndipo ngati mwamuna kapena mkazi ali ndi zikanga pa khungu la thupi lake, zikanga zoyerayera; wansembe aziona; ndipo taonani ngati zikanga zili pa khungu la thupi lao zikhala zotuwatuwa; ndilo thuza labuka pakhungu; ndiye woyera. Ndipo ngati tsitsi la munthu lathothoka, ndiye wadazi; koma woyera. Ndipo ngati tsitsi lathothoka pamphumi pake ndiye wa masweswe, koma woyera. Koma ngati pali nthenda yotuuluka pakati pa dazi lake la pamutu, kapena la pamphumi, ndipo khate lilikubuka pakati pa dazi lake la pamutu, kapena la pamphumi. Pamenepo wansembe azimuona, ndipo taonani, ngati chotupa chake cha nthenda chili chotuuluka pa dazi la pa mutu wake, kapena la pamphumi pake, monga maonekedwe a khate pa khungu la thupi; ndiye wakhate, ndiye wodetsedwa; wansembe amutchetu wodetsedwa; nthenda yake ili pamutu pake. Ndipo azing'amba zovala zake za wakhate ali ndi nthendayo, ndi tsitsi la pamutu pake lizikhala lomasuka, naphimbe iye mlomo wake wa m'mwamba, nafuule, Wodetsedwa, wodetsedwa! Masiku onse nthenda ikali pa iye azikhala wodetsedwa; ali wodetsedwa, agone pa yekha pokhala pake pakhale kunja kwa chigono. Ndiponso ngati nthenda yakhate ili pa chovala chaubweya, kapena chathonje; ngakhale ili pamuyaro, kapena pamtsendero, chathonje, kapena chaubweya, ngakhale ili pa chikopa, kapena pa chinthu chilichonse chopanga ndi chikopa; ngati nthenda ili yobiriwira, kapena yofiira pachovala, kapena pachikopa, kapena pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa, ndiyo nthenda yakhate; aziionetsa kwa wansembe; ndipo wansembe aone nthendayo, nabindikiritse chija cha nthenda masiku asanu ndi awiri; naone nthenda tsiku lachisanu ndi chiwiri; ngati nthenda yakula pachovala, ngakhale pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pachikopa, zilizonse zantchito zopangika ndi chikopa; nthendayo ndiyo khate lofukuta; ndicho chodetsedwa. Ndipo atenthe chovalacho ngakhale muyaro wake, ngakhale mtsendero wake, chaubweya kapena chathonje, kapena chilichonse chachikopa chili ndi khate, ndilo khate lofetsa; achitenthe ndi moto. Ndipo wansembe akaona, ndipo taonani, nthenda njosakula pachovala, kapena pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa; pamenepo wansembe aziuza kuti atsuke chija pali khate, nachibindikiritse masiku asanu ndi awiri ena; ndipo wansembe aone nthenda ataitsuka, ndipo taonani, ngati nthendayi siinasandulika maonekedwe ake, yosakulanso nthenda, ndicho chodetsedwa; uchitenthe ndi moto; ndilo funka, kungakhale kuyera kwake kuli patsogolo kapena kumbuyo. Ndipo wansembe akaona, ndipo taonani, nthenda yazimba ataitsuka, pamenepo aikadzule pa chovala, kapena chikopa, kapena muyaro, kapena mtsendero; ndipo ikaonekabe pachovala, ngakhale pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa, ilikubukanso; uchitenthe ndi moto chija chanthenda. Ndipo ukatsuka chovalacho, kapena muyaro, kapena mtsendero, kapena chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa, ngati nthenda yalekapo pa chimenecho, achitsukenso kawiri, pamenepo chili choyera. Ichi ndi chilamulo cha nthenda yakhate ili pa chovala chaubweya kapena chathonje, ngakhale pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa; kuchitcha choyera kapena kuchitcha chodetsa. Ndipo Yehova ananena ndi Mose nati, Chilamulo cha wakhate tsiku la kumyeretsa kwake ndi ichi: azidza naye kwa wansembe; ndipo wansembe atuluke kunka kunja kwa chigono; ndipo wansembe aone, ndipo taonani, ngati nthenda yakhate yapola pa wakhateyo; pamenepo wansembe auze kuti amtengere iye wakuti akonzedwe, mbalame ziwiri zoyera zamoyo, ndi mtengo wamkungudza, ndi ubweya wofiira, ndi hisope; ndipo wansembe auze kuti aphe mbalame imodzi m'mbale yadothi pamwamba pa madzi oyenda; natenge mbalame yamoyo, ndi mtengo wamkungudza, ndi ubweya wofiira, ndi hisope, naziviike pamodzi ndi mbalame yamoyo m'mwazi wa mbalame adaipha pamwamba pa madzi oyenda; nawaze kasanu ndi kawiri iye amene akuti amyeretse khate lake, namutche woyera, nataye mbalame yamoyo padambo poyera. Ndipo iye wakuti ayeretsedwe atsuke zovala zake, namete tsitsi lake lonse, nasambe madzi, nakhale woyera; ndipo atatero alowe kuchigono, koma agone pa bwalo la hema wake masiku asanu ndi awiri. Ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri kudzakhala kuti amete tsitsi lake lonse la pamutu pake, ndi ndevu zake, ndi nsidze zake, inde amete tsitsi lake lonse; natsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi, nakhale woyera. Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu atenge anaankhosa awiri, amuna opanda chilema, ndi mwanawankhosa mmodzi wamkazi wa chaka chimodzi wopanda chilema, ndi atatu a magawo khumi a efa la ufa wosalala ukhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndi muyeso umodzi wa magawo atatu wa mafuta. Ndipo wansembe amene amyeretsayo, amuike munthu uja wakuti ayeretsedwe, ndi zinthu zija, pamaso pa Yehova, pa khomo la chihema chokomanako; ndipo wansembe atenge mwanawankhosa mmodzi wamwamuna, nabwere naye akhale nsembe yopalamula, pamodzi ndi muyeso uja wa mafuta, naziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova. Ndipo akaphere mwanawankhosa wamwamuna paja amapherapo nsembe yauchimo, ndi nsembe yopsereza, pa malo popatulika; pakuti monga nsembe yauchimo momwemo nsembe yopalamula nja wansembe; ndiyo yopatulika kwambiri. Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yopalamula, ndipo wansembe aupake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lake lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja; ndipo wansembe atengeko muyeso uja wa mafuta, nawathire pa chikhato cha dzanja lake lamanzere la iye mwini; ndipo wansembe aviike chala chake cha dzanja lake lamanja cha iye mwini m'mafuta ali m'dzanja lake lamanzere, nawaze mafuta kasanu ndi kawiri ndi chala chake pamaso pa Yehova; ndipo wansembe apakeko mafuta okhala m'dzanja lake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lake lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja, pa mwazi wa nsembe yopalamula; natsitsitize mafuta otsala m'dzanja lake la wansembe, pamutu pa iye wakuti ayeretsedwe; ndipo wansembe amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova. Ndipo wansembe apereke nsembe yauchimo, namchitire chomtetezera amene akuti ayeretsedwe, chifukwa cha kudetsedwa kwake; ndipo atatero aphe nsembe yopsereza; ndipo wansembe atenthe nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa pa guwa la nsembe; ndipo wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhala iye woyera. Ndipo akakhala waumphawi chosafikana chuma chake azitenga mwanawankhosa mmodzi wamwamuna akhale nsembe yopalamula, aiweyule kumchitira chomtetezera, ndi limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa, ndi muyeso umodzi magawo atatu wa mafuta; ndi njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, monga akhoza kufikana; limodzi likhale la nsembe yauchimo, ndi linzake la nsembe yopsereza. Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu abwere nao kwa wansembe, ku khomo la chihema chokomanako, pamaso pa Yehova, kuti ayeretsedwe. Ndipo wansembe atenge mwanawankhosa wa nsembe yopalamula, ndi muyeso uja wa mafuta, ndipo wansembe aziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; naphe mwanawankhosa wa nsembe yopalamula, ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yopalamula, naupake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye akuti ayeretsedwe, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lake lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja; ndipo wansembe athireko mafuta aja m'chikhato chake chamanzere cha iye mwini; ndipo wansembe awazeko mafuta aja ali m'dzanja lake lamanzere ndi chala chake cha dzanja lamanja, kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova; ndipo wansembe apakeko mafuta aja ali m'dzanja lake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lake lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja, pa malo paja pali mwazi wa nsembe yopalamula; ndipo mafuta otsala m'dzanja la wansembe atsitsitize pa mutu wa iye wakuti ayeretsedwe, kumchitira chomtetezera pamaso pa Yehova. Ndipo iye apereke imodzi ya njiwazo, kapena limodzi la maunda, monga akhoza kufikana nazo, limodzi la nsembe yauchimo, ndi lina la nsembe yopsereza, pamodzi ndi nsembe yaufa; ndipo wansembe amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova iye wakuyeretsedwa. Ichi ndi chilamulo cha iye ali ndi nthenda yakhate, wosakhoza kufikana nazo zofunika pomyeretsa pake. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati, Mutakafika m'dziko la Kanani, limene ndikupatsani likhale lanulanu, ndipo ndikaika nthenda yakhate m'nyumba ya dziko lanulanu; pamenepo mwini nyumbayo adzauze wansembe, kuti, Ndiyesa muli ngati nthenda m'nyumba. Ndipo wansembe aziuza kuti atulutse zonse za m'nyumba, asanalowe kudzaona nthendayi, zinthu zonse zili m'nyumba zingakhale zodetsedwa; ndipo atatero wansembe alowe kukaona nyumbayi; naone nthendayo, ndipo taonani, nthenda ikakhala yosumbudzuka m'makoma a nyumba yobiriwira kapena yofiira, ndipo maonekedwe ake yakumba kubzola khoma; pamenepo wansembe azituluka ku khomo la nyumba, natseka nyumbayo masiku asanu ndi awiri; ndipo wansembe abwerenso tsiku lachisanu ndi chiwiri, naonenso, ndipo taonani, ngati nthenda yakula m'makoma a nyumba; pamenepo wansembe auze kuti agumule miyalayi pali nthenda, naitayire ku malo akuda kunja kwa mudzi; napalitse nyumba m'kati monsemo, natayire ku malo akuda kunja kwa mudzi dothi adapalako; natenge miyala ina, naikhazike m'malo mwa miyala ija; natenge dothi lina, namatenso nyumbayo. Ndipo ikabweranso nthenda, nibukanso m'nyumba atagumula miyala, ndipo atapala m'nyumba namatanso; pamenepo wansembe alowe naonemo, ndipo taonani, ngati nthenda yakula m'nyumba, ndiyo khate lonyeka m'nyumba; ndiyo yodetsedwa. Ndipo apasule nyumbayo, miyala yake, ndi mitengo yake, ndi dothi lake lonse kumudzi kuzitaya ku malo akuda. Ndiponso iye wakulowa m'nyumba masiku ake ili yotsekedwa, adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo. Ndipo iye wakugona m'nyumbayo atsuke zovala zake; ndi iye wakudya m'nyumbayo atsuke zovala zake. Ndipo wansembe akalowa, nakaona, ndipo taonani, nthenda siinakula m'nyumba, ataimata nyumba; wansembe aitche nyumbayo yoyera, popeza nthenda yaleka. Pamenepo atenge mbalame ziwiri, ndi mtengo wamkungudza, ndi ubweya wofiira, ndi hisope, kuti ayeretse nazo nyumbayo; naphe mbalame imodzi m'mbale yadothi, pamwamba pa madzi oyenda; natenge mtengo wamkungudza ndi hisope, ndi ubweya wofiira, ndi mbalame yamoyo, naziviike m'mwazi wa mbalame yakuphayo, ndi m'madzi oyenda, nawaze kasanu ndi kawiri m'nyumba; nayeretse nyumba ndi mwazi wa mbalame, ndi madzi oyenda, ndi mbalame yamoyo, ndi mtengo wamkungudza, ndi hisope, ndi ubweya wofiira. Koma ataye mbalame yamoyo kunja kwa mudzi kuthengo koyera; motero aichitire choitetezera nyumbayo; ndipo idzakhala yoyera. Ichi ndi chilamulo cha nthenda iliyonse yakhate, ndi yamfundu; ndi ya khate la chovala, ndi la nyumba; ndi yachotupa, ndi yankhanambo, ndi yachikanga; kulangiza tsiku loti chikhala chodetsa, ndi tsiku loti chikhala choyera; ichi ndi chilamulo cha khate. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati, Nenani nao ana a Israele, nimuti nao, Pamene mwamuna aliyense ali ndi nthenda yakukha m'thupi mwake, akhale wodetsedwa, chifukwa cha kukha kwake. Ndipo kudetsedwa kwa kukha kwake ndiko: ngakhale chakukhacho chituluka m'thupi mwake, ngakhale chaleka m'thupi mwake, ndiko kumdetsa kwake. Kama aliyense agonapo wakukhayo ali wodetsedwa; ndi chinthu chilichonse achikhalira chili chodetsedwa. Ndipo munthu aliyense wakukhudza kama wake azitsuka zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo. Ndipo iye wakukhalira chinthu chilichonse adachikhalira wakukhayo atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo. Ndipo iye wakukhudza thupi la uyo wakukhayo atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo. Ndipo wakukhayo akalavulira wina woyera; pamenepo atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo. Ndipo mbereko iliyonse akwerapo wakukhayo ili yodetsedwa. Ndipo munthu aliyense akakhudza kanthu kalikonse kadali pansi pake adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; ndipo iye wakunyamula zimenezo atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo. Ndipo munthu aliyense wakukhayo akamkhudza, osasambatu m'manja m'madzi, atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo. Ndipo zotengera zadothi wazikhudza wakukhayo, aziphwanye; ndi zamtengo, azitsuke ndi madzi. Ndipo wakukhayo atayeretsedwa ku kukha kwake, adziwerengere masiku asanu ndi awiri akhale a kuyeretsa kwake, natsuke zovala zake; nasambe thupi lake ndi madzi oyenda, nadzakhala woyera. Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu atenge njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, nafike pamaso pa Yehova pa khomo la chihema chokomanako, nazipereke kwa wansembe; ndipo wansembe azipereke izo, imodzi ikhale nsembe yauchimo, ndi ina nsembe yopsereza; ndipo wansembe amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova chifukwa cha kukha kwake. Ndipo munthu aliyense akagona uipa, azisamba thupi lake lonse ndi madzi, nadzakhala wodetsedwa kufukira madzulo. Ndipo chovala chilichonse, ndi chikopa chilichonse, anagona uipa pamenepo azitsuke ndi madzi, nizidzakhala zodetsedwa kufikira madzulo. Mkazi yemwe, mwamuna atagona naye, onse awiri asambe ndi madzi, nadzakhala odetsedwa kufikira madzulo. Ndipo ngati mkazi ali ndi nthenda yakukha, ndi kukha kwake nkwa mwazi m'thupi mwake, akhale padera masiku asanu ndi awiri; ndipo aliyense amkhudza adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo. Ndipo chinthu chilichonse agonapo pokhala ali padera nchodetsedwa; ndi chinthu chilichonse akhalapo nchodetsa. Ndipo aliyense akhudza kama wake azitsuka zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo. Ndipo aliyense akhudza chinthu chilichonse akhalapo iye, atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo. Ndipo chikakhala pakama, kapena pa chinthu chilichonse akhalapo iye, atachikhudza, adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo. Ndipo ngati mwamuna aliyense agona naye, ndi kudetsa kwake kukhala pa iye, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri; ndipo kama aliyense agonapo ali wodetsedwa. Ndipo mkazi akakhala ndi kukha mwazi masiku ambiri, osati masiku a kuoloka kwake, kapena akamakha kupitirira nthawi ya kuoloka kwake; masiku onse chilinkukha chomdetsa chake, adzakhala wodetsedwa, monga masiku a kuoloka kwake. Kama aliyense agonapo masiku a kukha kwake akhale ngati kama wa kuoloka kwake; ndi chinthu chilichonse akhalapo chili chodetsedwa, ngati kudetsa kwa kuoloka kwake. Ndipo munthu aliyense akakhudza zimenezi adzakhala wodetsedwa, natsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo. Koma akayeretsedwa kukha kwake, adziwerengere masiku asanu ndi awiri, ndipo atatero adzakhala woyeretsedwa. Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu atenge njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, nafike nazo kwa wansembe ku khomo la chihema chokomanako. Ndipo wansembe apereke limodzi likhale nsembe yauchimo, ndi linalo likhale nsembe yopsereza; ndipo wansembe amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova chifukwa cha kukha kwake komdetsa. Motero muzipatula ana a Israele kwa kudetsedwa kwao; angafe m'kudetsedwa kwao, pamene adetsa Kachisi wanga ali pakati pao. Ichi ndi chilamulo cha wakukha, ndi cha iye wakugona uipa, kuti kumkhalitse wodetsedwa; ndi cha mkazi alinkudwala ndi kudetsedwa kwake, ndi cha iye alikukha kapena mwamuna, kapena mkazi, ndi cha iye agona ndi mkazi wodetsedwa. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, atamwalira ana amuna awiri a Aroni, muja anasendera pamaso pa Yehova, namwalira; ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni mbale wako, kuti asalowe nthawi zonse m'malo opatulika m'tseri mwa nsalu yotchinga, pali chotetezerapo chokhala palikasa, kuti angafe; popeza ndioneka mumtambo pachotetezerapo. Aroni azilowa pa bwalo la malo opatulika nazozo: ng'ombe yamphongo ikhale ya nsembe yauchimo, ndi nkhosa yamphongo ikhale ya nsembe yopsereza. Avale malaya a m'kati a bafuta wopatulika, nakhale nazo zovala za kumiyendo pathupi pake, nadzimangire m'chuuno ndi mpango wabafuta, navale nduwira yabafuta; izi ndi zovala zopatulika; potero asambe thupi lake ndi madzi, ndi kuvala izi. Ndipo ku khamu la ana a Israele atenge atonde awiri akhale a nsembe yauchimo, ndi nkhosa yamphongo imodzi ikhale ya nsembe yopsereza. Ndipo Aroni abwere nayo ng'ombe ya nsembe yauchimo, ndiyo yakeyake, nachite chodzitetezera iye yekha, ndi mbumba yake. Ndipo atenge mbuzi ziwirizo naziimike pamaso pa Yehova pakhomo pa chihema chokomanako. Ndipo Aroni ayese maere pa mbuzi ziwirizo; maere amodzi kwa Yehova, ndi amodzi kwa Azazele. Ndipo Aroni abwere nayo mbuzi imene adaigwera maere a Yehova, naiyese nsembe yauchimo. Koma mbuzi imene adaigwera maere a Azazele, aiike yamoyo pamaso pa Yehova, kuti achite nayo chotetezera, kuitumiza kuchipululu ikhale ya Azazele. Ndipo Aroni abwere nayo ng'ombe ya nsembe yauchimo, ndiyo yakeyake, nadzitetezere iye yekha, ndi mbumba yake, ndi kupha ng'ombe ya nsembe yauchimo ndiyo yakeyake; natenge mbale ya zofukiza yodzala ndi makala amoto, kuwachotsa pa guwa la nsembe, pamaso pa Yehova, ndi manja ake odzala ndi chofukiza chopera cha fungo lokoma, nalowe nayo m'tseri mwa nsalu yotchinga; naike chofukizacho pamoto pamaso pa Yehova, kuti mtambo wa chofukiza chiphimbe chotetezerapo chokhala pamboni, kuti angafe. Ndipo atengeko mwazi wa ng'ombeyo, ndi kuuwaza ndi chala chake pachotetezerapo, mbali ya kum'mawa; nawaze mwazi ndi chala chake chakuno cha chotetezerapo kasanu ndi kawiri. Pamenepo aiphe mbuzi ya nsembe yauchimo, ndiyo yophera anthu, nalowe nao mwazi wake m'tseri mwa nsalu yotchinga, nachite nao mwazi wake monga umo anachitira ndi mwazi wa ng'ombe, nauwaze pachotetezerapo ndi chakuno cha chotetezerapo; nachitire chotetezera malo opatulika, chifukwa cha kudetsedwa kwa ana a Israele, ndi chifukwa cha zolakwa zao, monga mwa zochimwa zao zonse; nachitire chihema chokomanako momwemo, chakukhala nao pakati pa zodetsa zao. Ndipo musakhale munthu m'chihema chokomanako pakulowa iye kuchita chotetezera m'malo opatulika, kufikira atuluka, atachita chotetezera yekha, ndi mbumba yake, ndi msonkhano wonse wa Israele. Ndipo atulukire guwa la nsembe lokhala pamaso pa Yehova ndi kulichitira chotetezera; natengeko mwazi wa ng'ombeyo, ndi mwazi wa mbuziyo, ndi kuupaka pa nyanga za guwa la nsembe pozungulira. Ndipo awazepo mwazi wina ndi chala chake kasanu ndi katatu; ndi kuliyeretsa ndi kulipatula kulichotsera zodetsa za ana a Israele. Ndipo atatha kuchitira chotetezera malo opatulika, ndi chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe, abwere nayo mbuzi yamoyo; ndipo Aroni aike manja ake onse awiri pamutu pa mbuzi yamoyo, ndi kuvomereza pa iyo mphulupulu zonse za ana a Israele, ndi zolakwa zao zonse, monga mwa zochimwa zao zonse; naike izi pamutu pa mbuziyo, ndi kuitumiza kuchipululu ndi dzanja la munthu wompangiratu, ndi mbuziyo isenze yokha mphulupulu zonsezo kunka nazo ku dziko la pa lokha; ndipo azitaya mbuziyo m'chipululu. Pamenepo Aroni alowe m'chihema chokomanako, navule zovala zabafuta zimene anazivala polowa m'malo opatulika, nazisiye komweko. Ndipo asambe thupi lake ndi madzi kumalo kopatulika, navale zovala zake, natuluke, napereke nsembe yopsereza yake, ndi nsembe yopsereza ya anthu, nachite chodzitetezera yekha ndi anthu. Ndipo atenthe mafuta a nsembe yauchimo pa guwa la nsembe. Ndipo iye amene anachotsa mbuzi ipite kwa Azazele atsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi, ndipo atatero alowenso kuchigono. Koma ng'ombe ya nsembe yauchimo, ndi mbuzi ya nsembe yauchimo, zimene mwazi wao analowa nao kuchita nao chotetezera m'malo opatulika, atuluke nazo kunja kwa chigono; natenthe ndi moto zikopa zao, ndi nyama zao, ndi chipwidza chao. Ndi iye amene anazitentha atsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi, ndipo atatero alowenso kuchigono. Ndipo lizikhala kwa inu lemba losatha; mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi la mweziwo, muzidzichepetsa, osagwira ntchito konse, kapena wa m'dziko, kapena mlendo wakukhala pakati panu; popeza tsikuli adzachitira inu chotetezera, kukuyeretsani; adzakuyeretsani, kukuchotserani zoipa zanu zonse pamaso pa Yehova. Likhale kwa inu Sabata lakupumula, kuti mudzichepetse; ndilo lemba losatha. Ndipo wansembe, amene anamdzoza ndi kumdzaza dzanja lake achite ntchito ya nsembe m'malo mwa atate wake, achite chotetezera, atavala zovala zabafuta, zovala zopatulikazo. Ndipo achite chotetezera malo opatulikatu, natetezere chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe; momwemo atetezerenso ansembe, ndi anthu onse a msonkhanowo. Ndipo ichi chikhale kwa inu lemba losatha, kuchita chotetezera ana a Israele, chifukwa cha zochimwa zao zonse, kamodzi chaka chimodzi. Ndipo anachita monga Yehova adauza Mose. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Nena ndi Aroni, ndi ana ake amuna, ndi ana a Israele onse, nuti nao, Ichi ndi chimene Yehova wauza, ndi kuti, Munthu aliyense wa mbumba ya Israele akapha ng'ombe, kapena mwanawankhosa, kapena mbuzi, m'chigono, kapena akaipha kunja kwa chigono, osadza nayo ku khomo la chihema chokomanako, kuti aipereke chopereka cha Yehova, ku bwalo la Kachisi wa Yehova; azimuyesa munthuyu wochimwira mwazi, wakhetsa mwazi; ndipo amsadze munthuyo kumchotsa pakati pa anthu a mtundu wake; kotero kuti ana a Israele azidza nazo nsembe zao, zimene aziphera kuthengo koyera, kuti adze nazo kwa Yehova, ku khomo la chihema chokomanako, kwa wansembe, ndi kuziphera nsembe zoyamika za Yehova. Ndipo wansembeyo awaze mwaziwo pa guwa la nsembe la Yehova, pa khomo la chihema chokomanako, natenthe mafuta akhale fungo lokoma lokwera kwa Yehova. Ndipo asamapheranso milungu ina nsembe zao, zimene azitsata ndi chigololo. Ili liwakhalire lemba losatha mwa mibadwo yao. Ndipo uzinena nao, Munthu aliyense wa mbumba ya Israele, kapena mlendo wakugonera pakati panu, amene apereka nsembe yopsereza kapena nsembe yophera, osadza nayo ku khomo la chihema chokomanako, kuiphera Yehova; amsadze munthuyu kumchotsa kwa anthu a mtundu wake. Ndipo munthu aliyense wa mbumba ya Israele, kapena mlendo wogonera pakati panu, wakudya mwazi uliwonse; nkhope yanga idzatsutsana naye munthu wakudya mwaziyo, ndi kumsadza kumchotsa kwa anthu a mtundu wake. Pakuti moyo wa nyama ukhala m'mwazi; ndipo ndakupatsani uwu pa guwa la nsembe, uchite chotetezera moyo wanu; pakuti wochita chotetezera ndiwo mwazi, chifukwa cha moyo wake. Chifukwa chake ndinanena kwa ana a Israele, Asamadya mwazi mmodzi yense wa inu, kapena mlendo aliyense wakugonera mwa inu asamadya mwazi. Ndipo munthu aliyense wa ana a Israele, kapena mlendo wakugonera pakati pa inu, akasaka nyama kapena mbalame yakudya, nakaigwira; azikhetsa mwazi wake, naufotsere ndi dothi. Pakuti ndiwo moyo wa nyama zonse, mwazi wake ndiwo moyo wake; chifukwa chake ndinanena kwa ana a Israele, Musamadya mwazi wa nyama iliyonse; pakuti moyo wa nyama yonse ndi mwazi wake; aliyense akaudya adzasadzidwa. Ndipo aliyense wakudya yakufa yokha, kapena yojiwa kuthengo, ngakhale ndiye wa m'dziko kapena mlendo, azitsuka nsalu zake, nasambe ndi madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; pamenepo adzakhala woyera. Koma akapanda kuzitsuka, kapena kusamba thupi lake, adzasenza mphulupulu yake. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Ine ndine Yehova Mulungu wanu. Musamachita monga mwa machitidwe a dziko la Ejipito, muja munakhalamo; musamachita monga mwa machitidwe a dziko la Kanani kumene ndipita nanuko, nimusamayenda m'malemba ao. Muzichita maweruzo anga, ndi kusunga malemba anga, kumayenda m'mwemo; Ine ndine Yehova Mulungu wanu. Inde, muzisunga malemba anga, ndi maweruzo anga; amenewo munthu akawachita, adzakhala nao ndi moyo; Ine ndine Yehova. Asasendere mmodzi wa inu kwa mbale wake kumvula; Ine ndine Yehova. Usamavula atate wako, ndi mai wako; ndiye mai wako, usamamvula. Usamavula mkazi wa atate wako; ndiye thupi la atate wako. Usamavula mlongo wako, mwana wamkazi wa atate wako, kapena mwana wamkazi wa mai wako, wobadwa kwanu, kapena wobadwa kwina. Usamavula mwana wamkazi wa mwana wamwamuna wako, kapena mwana wamkazi wa mwana wamkazi wako; pakuti thupi lao ndi lako. Usamavula mwana wamkazi wa mkazi wa atate wako, amene anambala atate wako, ndiye mlongo wako. Usamavula mlongo wa atate wako; ndiye wa chibale cha atate wako. Usamavula mbale wa mai wako; popeza ndiye mbale wa mai wako. Usamavula mbale wa atate wako; usamasendera kwa mkazi wake; ndiye mai wako. Usamavula mpongozi wako; ndiye mkazi wa mwana wamwamuna wako; usamamvula. Usamavula mkazi wa mbale wako; ndiye thupi la mbale wako. Usamavula mkazi ndi mwana wamkazi wake; usamatenga mwana wamkazi wa mwana wamwamuna wake, kapena mwana wamkazi wa mwana wamkazi wake kumvula; ndiwo abale; chochititsa manyazi ichi. Usamtenga mkazi kumuonjezera kwa mbale wake, kumvuta, kumvula pamodzi ndi mnzake, akali ndi moyo mnzakeyo. Usamasendera kwa mkazi kumvula pokhala ali padera chifukwa cha kudetsedwa kwake. Usagona naye mkazi wa mnansi wako, kudetsedwa naye limodzi. Ndipo usamapereka a mbumba yako kuwapitiriza kumoto chifukwa cha Moleki; usamaipsa dzina la Mulungu wako; Ine ndine Yehova. Usamagonana ndi mwamuna, monga amagonana ndi mkazi; chonyansa ichi. Ndipo usamagonana ndi nyama iliyonse, kudetsedwa nayo; kapena mkazi asamaima panyama, kugonana nayo; chisokonezo choopsa ichi. Musamadzidetsa nacho chimodzi cha izi; pakuti amitundu amene ndiwapirikitsa pamaso panu amadetsedwa nazo zonsezi; dziko lomwe lidetsedwa; chifukwa chake ndililanga, ndi dzikoli lisanza okhala m'mwemo. Koma inu, muzisunga malemba anga ndi maweruzo anga, osachita chimodzi chonse cha zonyansa izi; ngakhale wa m'dziko ngakhale mlendo wakugonera pakati pa inu. (Pakuti eni dziko okhalako, musanafike inu, anazichita zonyansa izi zonse, ndi dziko linadetsedwa) lingakusanzeni inunso dzikoli, polidetsa inu, monga linasanza mtundu wa anthu wokhalako musanafike inu. Pakuti aliyense akachita chilichonse cha zonyansa izi, inde amene azichita adzasadzidwa pakati pa anthu a mtundu wao. Potero muzisunga chilangizo changa, ndi kusachita zilizonse za miyambo yonyansayi anaichita musanafike inu, ndi kusadzidetsa nayo: Ine ndine Yehova Mulungu wako. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Nena ndi khamu lonse la ana a Israele, nuti nao, Muzikhala oyera; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, ndine woyera. Aliyense aope mai wake, ndi atate wake; nimusunge masabata anga; Ine ndine Yehova Mulungu wanu. Musamatembenukira mafano, kapena kudzipangira mulungu woyenga; Ine ndine Yehova Mulungu wanu. Ndipo pamene muphera Yehova nsembe yoyamika, muiphere kuti mulandiridwe. Tsiku lomwelo mwaipha, ndi m'mawa mwake muidye; ngati katsalirako kanthu tsiku lachitatu, muzikatentha ndi moto. Akakadya konse tsiku lachitatu kali chonyansa, kosavomerezeka: koma aliyense akudyako adzasenza mphulupulu yake, popeza waipsa chopatulidwa cha Yehova; ndi munthuyu amsadze, kumchotsa kwa anthu a mtundu wake. Pakukolola dzinthu za m'dziko mwanu, usamakololetsa m'mphepete mwa munda wako, nusamakunkha khunkha. Usamakunkha khunkha la m'munda wako wamphesa, usamazitola zidagwazi za m'munda wako wamphesa; uzisiyire wosauka ndi mlendo; Ine ndine Yehova Mulungu wanu. Musamaba, kapena kunyenga, kapena kunamizana. Musamalumbira monama ndi kutchula dzina langa, ungaipse dzina la Mulungu wako; Ine ndine Yehova. Usamasautsa mnansi wako, kapena kulanda zake; mphotho yake ya wolipidwa isakhale ndi iwe kufikira m'mawa. Usamatemberera wogontha; usamaika chokhumudwitsa pamaso pa wosaona; koma uziopa Mulungu wako; Ine ndine Yehova. Musamachita chisalungamo pakuweruza mlandu; usamavomereza munthu wosauka, kapena kulemekeza munthu womveka; uweruze mlandu wa munthu mnzako molungama. Usamayendayenda nusinjirira mwa anthu a mtundu wako; usamatsata mwazi wa mnansi wako; Ine ndine Yehova. Usamamuda mbale wako mumtima mwako; umdzudzule munthu mnzako ndithu, usadzitengera uchimo chifukwa cha iye. Usamabwezera chilango, kapena kusunga kanthu kukhosi pa ana a anthu a mtundu wako; koma uzikonda mnansi wako monga udzikonda wekha; Ine ndine Yehova. Muzisunga malemba anga. Usamalola zoweta zako za mitundu yosiyana zikwerane; usamabzala m'munda mwako mbeu za mitundu iwiri; usamavala chovala cha nsalu za mitundu iwiri zosokonezana. Munthu akagona ndi mkazi, ndiye mdzakazi, wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, wosamuombola kapena wosapatsidwa ufulu, akwapulidwe; asawaphe, popeza si mfulu mkaziyo. Ndipo adze nayo nsembe yake yopalamula kwa Yehova, ku khomo la chihema chokomanako, ndiyo nkhosa yamphongo ikhale nsembe yopalamula. Ndipo wansembe achite chomtetezera ndi nkhosa yamphongo ya nsembe yopalamula pamaso pa Yehova, chifukwa cha kuchimwa adachimwaku; ndipo adzakhululukidwa chifukwa cha kuchimwa kwake adachimwaku. Ndipo mukadzalowa m'dzikomo, ndi kubzala mitengo ya mitundumitundu ikhale ya chakudya, muziyese zipatso zao monga kusadulidwa kwao; zaka zitatu muziyese zosadulidwa; zisadyedwa. Koma chaka chachinai zipatso zake zonse zikhale zopatulika, za kumlemekeza nazo Yehova. Chaka chachisanu muzidya zipatso zake, kuti zobala zake zikuchulukireni inu; Ine ndine Yehova Mulungu wanu. Musamadya kanthu ndi mwazi wake; musamachita nyanga, kapena kuombeza ula. Musamameta mduliro, kapena kumeta m'mphepete mwa ndevu zanu. Musamadzicheka matupi anu chifukwa cha akufa, kapena kutema mphini; Ine ndine Yehova. Usamaipsa mwana wako wamkazi ndi kumchititsa chigololo; lingadzale ndi chigololo dzikoli, ndi kudzazidwa nazo zochititsa manyazi. Muzisunga masabata anga, ndi kuchitira ulemu malo anga opatulika; Ine ndine Yehova. Musamatembenukira kwa obwebweta, kapena anyanga; musawafuna, ndi kudetsedwa nao; Ine ndine Yehova Mulungu wanu. Pali aimvi uziwagwadira, nuchitire ulemu munthu wokalamba; nuope Mulungu wako; Ine ndine Yehova. Ndipo mlendo akagonera m'dziko mwanu, musamamsautsa. Mlendo wakugonera kwa inu mumuyese pakati pa inu monga wa m'dziko momwemo; umkonde monga udzikonda wekha; popeza munali alendo m'dziko la Ejipito; Ine ndine Yehova Mulungu wanu. Musamachita chisalungamo poweruza mlandu, poyesa utali wake, kulemera kwake, kapena kuchuluka kwake. Mukhale nacho choyesera choona, miyeso yoona, efa woona, hini woona; Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani m'dziko la Ejipito. Ndipo musamalire malemba anga onse, ndi maweruzo anga onse, ndi kuwachita; Ine ndine Yehova. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Unenenso kwa ana a Israele ndi kuti, Aliyense wa ana a Israele, kapena wa alendo akukhala m'Israele, amene apereka mbeu zake kwa Moleki, azimupha ndithu; anthu a m'dziko amponye miyala. Ndipo nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndi kumsadza kumchotsa pakati pa anthu a mtundu wake; popeza anapereka a mbeu zake kwa Moleki, kudetsa nako malo anga opatulika, ndi kuipsa dzina langa lopatulika. Ndipo ngati anthu a m'dzikomo akambisa munthuyo pang'ono ponse, pamene apereka a mbeu zake kwa Moleki, kuti asamuphe; pamenepo nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndi banja lake, ndi kumsadza iye, ndi onse akumtsata ndi chigololo kukachita chigololo kwa Moleki, kuwachotsa pakati pa anthu a mtundu wao. Ndipo munthu wakutembenukira kwa obwebweta ndi anyanga kuwatsata ndi chigololo, nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndipo ndidzamsadza kumchotsa pakati pa anthu a mtundu wake. Chifukwa chake dzipatuleni, nimukhale oyera; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu. Ndipo musunge malemba anga ndi kuwachita; Ine ndine Yehova wakupatula inu. Pakuti aliyense wakutemberera atate wake kapena mai wake azimupha ndithu; watemberera atate wake kapena amai wake; mwazi wake ukhale pamutu pake. Munthu akachita chigololo ndi mkazi wa mwini, popeza wachita chigololo ndi mkazi wa mnansi wake, awaphe ndithu, mwamuna ndi mkazi onse awiri. Munthu akagona naye mkazi wa atate wake, wavula atate wake; awaphe ndithu onse awiri; mwazi wao ukhale pamutu pao. Munthu akagona ndi mpongozi wake, awaphe onse awiri; achita chisokonezo; mwazi wao ukhale pamtu pao. Munthu akagonana ndi mwamuna mnzake, monga amagonana ndi mkazi, achita chonyansa onse awiri; awaphe ndithu; mwazi wao ukhale pamtu pao. Munthu akatenga mkazi pamodzi ndi mai wake chochititsa manyazi ichi; aziwatentha ndi moto, iye ndi iwowa; kuti pasakhale chochititsa manyazicho pakati pa inu. Mwamuna akagona ndi nyama amuphe ndithu; muiphenso nyamayi. Mkazi akasendera kwa nyama iliyonse kugonana nayo, umuphe mkaziyo, ndi nyama yomwe; muwaphe ndithu; mwazi wao ukhale pamtu pao. Munthu akatenga mlongo wake, mwana wamkazi wa atate wake, kapena mwana wamkazi wa mai wake, nakaona thupi lake, ndi mlongoyo akaona thupi lake; chochititsa manyazi ichi; ndipo awasadze pamaso pa ana a anthu ao; anavula mlongo wake; asenze mphulupulu yake. Munthu akagona ndi mkazi ali mumsambo, nakamvula, anavula kasupe wake, ndi iye mwini anavula kasupe wa nthenda yake; awadule onse awiri pakati pa anthu a mtundu wao. Usamavula mbale wa mai wako, kapena mlongo wa atate wako; popeza anavula abale ake; asenze mphulupulu yao. Munthu akagona ndi mkazi wa mbale wa atate wake, navula mbale wa atate wake; asenze kuchimwa kwao; adzafa osaona ana. Munthu akatenga mkazi wa mbale wake, chodetsa ichi; wavula mbale wake; adzakhala osaona ana. Potero muzisunga malemba anga onse, ndi maweruzo anga onse, kuwachita; lingakusanzeni inu dziko limene ndipita nanuko, kuti mukhale m'mwemo. Musamatsata miyambo ya mtundu umene ndiuchotsa pamaso panu; popeza anachita izi zonse, ndinalema nao. Koma ndanena nanu, Mudzalandira dziko lao inu, ndipo Ine ndilipereka kwa inu likhale lanu, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakusiyanitsani ndi mitundu ina ya anthu. Potero musiyanitse pakati pa nyama zoyera ndi nyama zodetsa, ndi pakati pa mbalame zodetsa ndi zoyera; ndipo musadzinyansitsa ndi nyama, kapena mbalame, kapena ndi kanthu kalikonse kakukwawa pansi, kamene ndinakusiyanitsirani kakhale kodetsa. Ndipo muzikhala oyera kwa Ine; pakuti Ine Yehova ndine woyera, ndipo ndinakusiyanitsani kwa mitundu ya anthu mukhale anga. Munthu wamwamuna kapena wamkazi wakubwebweta, kapena wanyanga, azimupha ndithu; aziwaponya miyala; mwazi wao ukhale pamtu pao. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Nena ndi ansembe, ana a Aroniwo, nuti nao, Asadzidetse mmodzi wa inu chifukwa cha wakufa mwa anthu a mtundu wake; koma chifukwa cha abale ake enieni ndiwo, mai wake, ndi atate wake, ndi mwana wake wamwamuna, ndi mwana wake wamkazi, ndi mbale wake; ndi chifukwa cha mlongo wake weniweni, akakhala namwali wosakhala naye mwamuna, nkuloleka adzidetse chifukwa cha iwowa. Akakhala mwini banja pakati pa anthu a mtundu wake, asadzidetse, ndi kudziipsa. Asamete tsitsi la pamtu pao, kapena kuchecherera ndevu zao, kapena kudzicheka matupi ao. Azikhala opatulikira Mulungu wao, osaipsa dzina la Mulungu wao; popeza amapereka nsembe zamoto za Yehova, mkate wa Mulungu wao; chifukwa chake akhale opatulika. Asadzitengere mkazi wachigololo, kapena woipsidwa; asatenge mkazi woti adamchotsa mwamuna wake; popeza apatulikira Mulungu wake. Chifukwa chake umpatule; popeza amapereka mkate wa Mulungu wako; umuyese wopatulika; pakuti Ine Yehova wakupatula iwe, ndine woyera, Akadziipsa mwana wamkazi wa wansembe ndi kuchita chigololo, alikuipsa atate wake, amtenthe ndi moto. Ndipo iye wokhala mkulu wansembe mwa abale ake, amene anamtsanulira mafuta odzoza pamutu pake, amene anamdzaza dzanja kuti avale zovalazo, asawinde, kapena kung'amba zovala zake. Asafike kuli mtembo; asadzidetse chifukwa cha atate wake, kapena mai wake. Asatuluke m'malo opatulika, kapena kuipsa malo opatulika a Mulungu wake; popeza korona wa mafuta odzoza wa Mulungu wake ali pa iye; Ine ndine Yehova. Ndipo adzitengere mkazi akali namwali. Mkazi wamasiye, kapena womleka, kapena woipsidwa, wachigololo, oterewa asawatenge; koma azitenga namwali wa anthu a mtundu wake akhale mkazi wake. Asaipse mbeu yake mwa anthu a mtundu wake; popeza Ine ndine Yehova wakumpatula iye. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Nena ndi Aroni, kuti, Aliyense wa mbeu zako mwa mibadwo yao wakukhala nacho chilema, asayandikize kupereka mkate wa Mulungu wake. Pakuti munthu aliyense wokhala nacho chilema, asayandikize; wakhungu, kapena wotsimphina, kapena wopunduka mphuno, kapena wamkulu chiwalo, kapena munthu wopunduka phazi kapena wopunduka dzanja, kapena wowerama, kapena wamfupi msinkhu, kapena wopunduka diso, kapena munthu wamphere, kapena wachipere, kapena wopunduka kumoto. Wa mbeu ya Aroni wansembe asayandikize mmodzi wokhala nacho chilema, kupereka nsembe zamoto za Yehova; ali nacho chilema asayandikize kupereka chakudya cha Mulungu wake. Adye chakudya cha Mulungu wake, chopatulika kwambiri, ndi chopatulika; koma asafike ku nsalu yotchinga, asayandikize ku guwa la nsembe, popeza ali nacho chilema; kuti angaipse malo anga opatulika; popeza Ine ndine Yehova wakuwapatula. Momwemo Mose ananena ndi Aroni, ndi ana ake amuna, ndi ana onse a Israele. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Nena ndi Aroni ndi ana ake amuna, kuti azikhala padera ndi zinthu zopatulika za ana a Israele, zimene amandipatulira Ine, ndipo asaipse dzina langa loyera; Ine ndine Yehova. Nena nao, Aliyense wa mbeu zanu zonse mwa mibadwo yanu, akayandikiza zinthu zopatulika, zimene ana a Israele azipatulira Yehova, pokhala ali nacho chomdetsa chake, azimsadza munthuyo pankhope panga; Ine ndine Yehova. Munthu aliyense wa mbeu za Aroni wokhala ndi khate, kapena kukha, asadyeko zinthu zopatulika, kufikira atayera. Ndipo aliyense wokhudza chinthu chodetsedwa ndi wakufa, kapena mwamuna wogona uipa; ndi aliyense wokhudza chinthu chokwawa chakudetsedwa nacho, kapenanso munthu amene akamdetsa nacho, chodetsa chake chilichonse; munthu wokhudza chilichonse chotere adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo, ndipo asadye zinthu zopatulika, akapanda kusamba thupi lake ndi madzi. Koma litalowa dzuwa, adzakhala woyera, ndi pambuyo pake adyeko zoyerazo, popeza ndizo chakudya chake. Asamadya zakufa zokha, kapena zojiwa, kudzidetsa nazo; Ine ndine Yehova. Potero asunge chilangizo changa, angasenzepo uchimo, ndi kufera m'mwemo, pakuchiipsa; Ine ndine Yehova wakuwapatula iwo. Mlendo asadyeko chopatulikacho; wakungokhala, ndi wansembe, kapena wolembedwa ntchito, asadyeko chopatulikacho. Koma wansembe atakagula munthu ndi ndalama zake, iyeyu adyeko; ndi iwo amene anabadwa m'nyumba yake, adyeko mkate wake. Ndipo mwana wamkazi wa wansembe akakwatibwa ndi mlendo, asadyeko nsembe yokweza ya zinthu zopatulika. Koma mwana wamkazi wa wansembe akakhala wamasiye kapena wochotsedwa, ndipo alibe mwana, nabwerera kunyumba ya atate wake, monga muja anali mwana, adyeko mkate wa atate wake; koma mlendo asamadyako. Ndipo munthu akadyako chinthu chopatulika mosadziwa, azionjezapo limodzi la magawo asanu, nalipereke kwa wansembe, pamodzi ndi chopatulikacho. Potero asaipse zinthu zopatulika za ana a Israele, zopereka iwo kwa Yehova; ndi kuwasenzetsa mphulupulu yakuwapalamulitsa, pakudya iwo zopatulika zao; pakuti Ine ndine Yehova wakuwapatula. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Nena ndi Aroni, ndi ana ake amuna, ndi ana onse a Israele, nuti nao, Aliyense wa mbumba ya Israele, kapena wa alendo ali m'Israele, akabwera nacho chopereka chake, monga mwa zowinda zao zonse, kapena monga mwa zopereka zaufulu zao, zimene abwera nazo kwa Yehova zikhale nsembe zopsereza; kuti mulandiridwe, azibwera nayo yaimuna yopanda chilema, ya ng'ombe, kapena nkhosa kapena mbuzi. Musamabwera nayo yokhala ndi chilema; popeza siidzalandirikira inu. Ndipo munthu akabwera nayo nsembe yoyamika kwa Yehova, ya pa chowinda chachikulu, kapena ya pa chopereka chaufulu, ya ng'ombe kapena nkhosa, ikhale yangwiro kuti ilandirike; ikhale yopanda chilema. Musamabwera nazo kwa Yehova yakhungu, kapena yoduka mwendo, kapena yopunduka, kapena yafundo, kapena yausemwe, kapena ya usemwe waukulu, musamazipereka kwa Yehova nsembe zamoto pa guwa la nsembe. Ng'ombe kapena nkhosa yokula kapena yochepa chiwalo, ikhale nsembe yaufulu; koma pa chowinda siidzalandirika. Nyama yofula, kapena chopwanya kapena chosansantha, kapena chotudzula, kapena chodula, musamabwera nazo kwa Yehova; inde musamachita ichi m'dziko mwanu. Ndipo musamazilandira izi ku dzanja la mlendo ndi kubwera nazo zikhale chakudya cha Mulungu wanu; popeza zili nako kuvunda kwao; zili ndi chilema; sizidzalandirikira inu. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Zikamabadwa ng'ombe kapena nkhosa, kapena mbuzi, zikhale ndi make masiku asanu ndi awiri; kuyambira tsiku lachisanu ndi chitatu ndi m'tsogolo mwake, idzalandirika ngati chopereka nsembe yamoto ya Yehova. Koma musamaipha ng'ombe kapena nkhosa pamodzi ndi mwana wake tsiku limodzimodzi. Ndipo mukamaphera Yehova nsembe yoyamika, muiphere kuti mulandirike. Idyedwe tsiku lomwelo; musamasiyako kufikira m'mawa; Ine ndine Yehova. Potero muwasunge malamulo anga, ndi kuwachita; Ine ndine Yehova. Musamaipsa dzina langa loyera; koma ndikhale woyera pakati pa ana a Israele; Ine ndine Yehova wakukupatulani, amene ndinakutulutsani m'dziko la Ejipito, kuti ndikhale Mulungu wanu; Ine ndine Yehova. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Nyengo zoikika za Yehova zimene muzilalikira zikhale masonkhano opatulika, ndizo nyengo zanga zoikika. Masiku asanu ndi limodzi azigwira ntchito; koma lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata lakupumula, msonkhano wopatulika; musamagwira ntchito konse; ndilo Sabata la Yehova m'nyumba zanu zonse. Izi ndi nyengo zoikika za Yehova, masonkhano opatulika, zimene muzilalikira pa nyengo zoikika zao. Mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chinai la mweziwo, madzulo, pali Paska wa Yehova. Ndipo tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi womwewo ndilo chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa a Yehova; masiku asanu ndi awiri muzidya mkate wopanda chotupitsa. Tsiku lake loyamba mukhale nao msonkhano wopatulika; musamagwira ntchito ya masiku ena. Koma mubwere nayo kwa Yehova nsembe yamoto masiku asanu ndi awiri; pa tsiku lachisanu ndi chiwiri pakhale msonkhano wopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mutakalowa m'dziko limene ndikupatsani, ndi kucheka dzinthu zake, pamenepo muzidza nao mtolo wa zipatso zoyamba za masika anu kwa wansembe; ndipo iye aweyule mtolowo pamaso pa Yehova, ulandirikire inu, tsiku lotsata Sabata wansembe aweyule. Ndipo tsiku loweyula mtolowo, ukonze mwanawankhosa wopanda chilema, wa chaka chimodzi, akhale nsembe yopsereza ya Yehova. Ndipo nsembe yaufa yake ikhale awiri a magawo khumi a efa wa ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, ndiyo nsembe yamoto ya Yehova, ichite fungo lokoma; ndi nsembe yake yothira ikhale yavinyo, limodzi la magawo anai la hini. Musamadya mkate, kapena tirigu wokazinga, kapena ngala zaziwisi, kufikira tsiku lomweli, kufikira mutadza nacho chopereka cha Mulungu wanu; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu m'nyumba zanu zonse. Ndipo mudziwerengere kuyambira tsiku lotsata Sabata, kuyambira tsikuli mudadza nao mtolo wansembe yoweyula; pakhale masabata asanu ndi awiri amphumphu; muwerenge masiku makumi asanu kufikira tsiku lotsata sabata lachisanu ndi chiwiri; pamenepo mubwere nayo kwa Yehova nsembe ya ufa watsopano. Mutuluke nayo m'zinyumba zanu mikate iwiri ya nsembe yoweyula, ikhale ya awiri a magawo khumi a efa; ikhale ya ufa wosalala, yopanga ndi chotupitsa, zipatso zoyamba za Yehova. Ndipo mubwere nao pamodzi ndi mikate, anaankhosa asanu ndi awiri, opanda chilema a chaka chimodzi, ndi ng'ombe yamphongo imodzi, ndi nkhosa zamphongo ziwiri; zikhale nsembe yopsereza ya Yehova, pamodzi ndi nsembe yao yaufa, ndi nsembe zao zothira, ndizo nsembe yamoto ya fungo lokoma la Yehova. Mukonzenso mwanawambuzi mmodzi akhale nsembe yauchimo, ndi anaankhosa awiri a chaka chimodzi akhale nsembe yoyamika. Ndi wansembe awaweyule, pamodzi ndi mkate wa zipatso zoyamba, nsembe yoweyula pamaso pa Yehova, pamodzi ndi anaankhosa awiriwo; zikhale zopatulikira Yehova, kuti zikhale za wansembe. Ndipo mulalikire tsiku lomwelo; kuti mukhale nao msonkhano wopatulika; musamagwira ntchito ya masiku ena; ndilo lemba losatha m'nyumba zanu zonse, mwa mibadwo yanu yonse. Ndipo pakukolola dzinthu za m'dziko mwanu, usamakololetsa m'mphepete mwa munda wako, nusamakunkha khunkha; uzisiyire wosauka ndi mlendo; Ine ndine Yehova Mulungu wako. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Nena ndi ana a Israele, ndi kuti, Mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku loyamba la mweziwo, muzipumula, ndiko chikumbutso cha kuliza malipenga, msonkhano wopatulika. Musamagwira ntchito ya masiku ena; mubwere nayo nsembe yamoto ya Yehova. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Komatu, tsiku lakhumi la mwezi uwu wachisanu ndi chiwiri, ndilo tsiku la chitetezero; mukhale nao msonkhano wopatulika, ndipo mudzichepetse; ndi kubwera nayo nsembe yamoto kwa Yehova. Musamagwira ntchito iliyonse tsiku limenelo; pakuti ndilo tsiku la chitetezero, kuchita chotetezera inu pamaso pa Yehova Mulungu wanu. Pakuti munthu aliyense wosadzichepetsa tsiku limenelo, amsadze kwa anthu a mtundu wake. Ndi munthu aliyense wakugwira ntchito iliyonse tsiku limenelo, ndidzaononga munthuyo pakati pa anthu a mtundu wake. Musamagwira ntchito iliyonse; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu, m'nyumba zanu zonse. Likhale ndi inu Sabata lakupumula; ndipo mudzichepetse; tsiku lachisanu ndi chinai madzulo, kuyambira madzulo kufikira madzulo musunge Sabata lanu. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Nena ndi ana a Israele, kuti, Tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi uno wachisanu ndi chiwiri pali chikondwerero cha Misasa ya Yehova, masiku asanu ndi awiri. Tsiku loyamba likhale msonkhano wopatulika, musamagwira ntchito ya masiku ena. Masiku asanu ndi awiri mubwere nayo nsembe yamoto kwa Yehova; tsiku lachisanu ndi chitatu mukhale nao msonkhano wopatulika; ndipo mubwere nayo nsembe yamoto kwa Yehova; ndilo lotsirizira; musamagwira ntchito ya masiku ena. Izi ndi nyengo zoikika za Yehova, zimene muzilalikira zikhale masonkhano opatulika, kukabwera nayo nsembe yamoto kwa Yehova, nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa, nsembe yophera, ndi nsembe yothira, yonse pa tsiku lakelake; pamodzi ndi masabata a Yehova, ndi pamodzi ndi mphatso zanu, ndi pamodzi ndi zowinda zanu zonse, ndi pamodzi ndi zopereka zaufulu zanu, zimene muzipereka kwa Yehova. Koma tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachisanu ndi chiwiri, mutatuta zipatso za m'dziko, muzisunga chikondwerero cha Yehova masiku asanu ndi awiri; tsiku loyamba mupumule, ndi tsiku lachisanu ndi chitatu mupumule. Ndipo tsiku loyambali mudzitengere nthambi za mitengo yokoma, nsomo za kanjedza, ndi nthambi za mitengo yovalira, ndi misondodzi ya kumtsinje; ndipo mukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu masiku asanu ndi awiri. Ndipo musunge chikondwerero cha Yehova masiku asanu ndi awiri m'chaka; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu; musunge mwezi wachisanu ndi chiwiri. Mukhale m'misasa masiku asanu ndi awiri; onse obadwa m'dziko mwa Israele akhale m'misasa; kuti mibadwo yanu ikadziwe kuti ndinakhalitsa ana a Israele m'misasa, pamene ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito; Ine ndine Yehova Mulungu wanu. Ndipo Mose anafotokozera ana a Israele nyengo zoikika za Yehova. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Uza ana a Israele, kuti akutengere mafuta a azitona oyera opera akuunikira, kuti aziwalitsa nyali nthawi zonse. Aroni aikonze kunja kwa nsalu yotchinga ya mboni, m'chihema chokomanako, kuyambira madzulo kufikira m'mawa, pamaso pa Yehova nthawi zonse; likhale lemba losatha mwa mibadwo yanu. Akonze nyalizo pa choikapo nyali choona pamaso pa Yehova nthawi zonse. Ndipo uzitenga ufa wosalala, ndi kuphika timitanda khumi ndi tiwiri; awiri a magawo khumi a efa afikane kamtanda kamodzi. Ndipo utiike m'mizere iwiri, tisanu ndi kamodzi mzere umodzi, pa gome loyera, pamaso pa Yehova. Nuike lubani loona ku mzere uliwonse, kuti likhale kumkate ngati chokumbutsa, nsembe yamoto ya Yehova. Nthawi zonse tsiku la Sabata aukonze pamaso pa Yehova, chifukwa cha ana a Israele, ndilo pangano losatha. Ndipo ukhale wa Aroni ndi ana ake, audye pamalo popatulika; pakuti auyese wopatulika kwambiri wochokera ku nsembe zamoto za Yehova; ndilo lemba losatha. Ndipo mwana wamwamuna wa mkazi Wachiisraele, atate wake ndiye Mwejipito, anatuluka mwa ana a Israele; ndi mwana wamwamuna wa mkazi Wachiisraeleyo analimbana naye munthu Mwisraele kuchigono; ndipo mwana wamwamuna wa mkazi Wachiisraele anachitira Dzina mwano, natemberera; ndipo anadza naye kwa Mose. Dzina la mai wake ndiye Selomiti, mwana wa Dibiri, wa fuko la Dani. Ndipo anamsunga m'kaidi, kuti awafotokozere m'mene anenere Yehova. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Tuluka naye wotembererayo kunja kwa chigono; ndipo onse adamumva aike manja ao pamutu pake, ndi khamu lonse limponye miyala afe. Ndipo unene ndi ana a Israele, ndi kuti, Aliyense wotemberera Mulungu wake azisenza kuchimwa kwake. Ndi iye wakuchitira mwano dzina la Yehova, amuphe ndithu; khamu lonse limponye miyala ndithu; mlendo ndi wobadwa m'dziko yemwe akachitira dzina la Yehova mwano, awaphe. Munthu akakantha munthu mnzake aliyense kuti afe, amuphe ndithu. Munthu akakantha nyama kuti ife, ambwezere ina; moyo kulipa moyo. Munthu akachititsa mnansi wake chilema, monga umo anachitira momwemo amchitire iye; kuthyola kulipa kuthyola, diso kulipa diso, dzino kulipa dzino; monga umo anachitira munthu chilema, momwemo amchitire iye. Iye wakukantha nyama kuti ife, ambwezere ina; iye wakupha munthu, amuphe. Chiweruzo chanu chifanefane ndi mlendo ndi wobadwa m'dziko; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu. Ndipo Mose ananena ndi ana a Israele, ndipo anatulutsa wotembererayo kunja kwa chigono, namponya miyala. Ndipo ana a Israele anachita monga Yehova adauza Mose. Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'phiri la Sinai, ndi kuti, Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mutakalowa m'dziko limene ndikupatsani, dzikoli lizisungira Yehova Sabata. Zaka zisanu ndi chimodzi ubzale m'munda mwako, ndi zaka zisanu ndi chimodzi udzombole mphesa zako, ndi kucheka zipatso zake; koma chaka chachisanu ndi chiwiri chikhale Sabata lakupumula la dziko, Sabata la Yehova; usamabzala m'munda mwako, usamadzombola mipesa yako. Zophuka zokha zofikira masika usamazithyola, ndi mphesa za mipesa yako yosadzombola usazicheka; chikhale chaka chopumula dziko. Ndipo Sabata la dzikoli likhale kwa inu la chakudya; kwa iwe, ndi mnyamata wako, ndi mdzakazi wako, ndi wolembedwa ntchito yako, ndi mlendo wako wakugonera kwanu; ndi ng'ombe zako, ndi nyama zili m'dziko lako; zipatso zake zonse zikhale chakudya chao. Ndipo uziwerengera masabata a zaka asanu ndi awiri, zaka zisanu ndi ziwiri kasanu ndi kawiri; kotero kuti zaka za masabata a zaka asanu ndi awiri, zifikire zaka makumi anai kudza zisanu ndi zinai. Pamenepo uzitumizira lipenga lomveka m'mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi la mweziwo; tsiku la chitetezero mutumizire lipenga lifikire m'dziko lanu lonse. Ndipo muchipatule chaka cha makumi asanu, ndi kulalikira kwa onse okhala m'dzikomo kuti akhale aufulu; muchiyese chaka choliza lipenga; ndipo mubwerere munthu aliyense ku zakezake, ndipo mubwerere yense ku banja lake. Muchiyese chaka cha makumi asanucho choliza lipenga, musamabzala, kapena kucheka zophuka zokha m'mwemo; kapena kucheka mphesa zake za mipesa yosadzombola. Popeza ndicho chaka choliza lipenga; muchiyese chopatulika, mudye zipatso zake kunja kwa munda. Chaka choliza lipenga ichi mubwerere nonse ku zakezake. Ndipo ukagulitsa kanthu kwa mnansi wako, kapena kugula kanthu ka mnansi wako, musamasautsana; monga mwa kuwerenga kwake kwa zaka, chitapita choliza lipenga, uzigula kwa mnansi wako, ndi monga mwa kuwerenga kwa zaka za zipatso azigulitsa. Monga mwa kuchuluka kwa zaka zake uonjeze mtengo wake, ndi monga mwa kuchepa kwa zaka zake uchepse mtengo wake; pakuti akugulitsa powerenga masiku ake. Musamasautsana, koma uope Mulungu wako; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wanu. M'mwemo muchite malemba anga, ndi kusunga maweruzo anga, ndi kuwachita; ndipo mudzakhala m'dzikomo okhazikika. Dziko lidzaperekanso zipatso zake, ndipo mudzadya ndi kukhuta, ndi kukhalamo okhazikika. Ndipo mukadzati, Tidzadyanji chaka chachisanu ndi chiwiri? Taonani, sitidzabzala, sitidzakolola dzinthu; pamenepo ndidzauza dalitso langa litsike pa inu chaka chachisanu ndi chimodzi, ndipo chidzapatsa zipatso zofikira zaka zitatu. Ndipo mubzale chaka chachisanu ndi chitatu, ndi kudya zipatso zasundwe; kufikira chaka chachisanu ndi chinai, mpaka zitacha zipatso zake mudzadya zasundwe. Ndipo asaligulitse dziko chigulitsire; popeza dzikoli ndi langa; pakuti inu ndinu alendo akugonera ndi Ine. Potero muzilola liomboledwe dziko lonse muli nalo. Mbale wako akasaukira chuma, nakagulitsa chakechake, pamenepo mombolo wake, mbale wake weniweni azidza, naombole chimene mbale wake anagulitsacho. Ndipo munthu akasowa mombolo, koma dzanja lake lachionetsa, nachipeza chofikira kuchiombola; pamenepo awerenge zaka za kugulitsa kwake, nabwezere wogulayo zotsalirapo nabwerere iye ku dziko lake. Koma dzanja lake likapanda kupeza zofikira za kumbwezera, pamenepo chogulitsacho chikhale m'dzanja lake la iye adachigulayo, kufikira chaka choliza lipenga; koma chaka choliza lipenga chituluke, nabwerere iye ku dziko lake. Munthu akagulitsa nyumba yogonamo, m'mudzi wa m'linga, aiombole chisanathe chaka choigulitsa; kufikira kutha chaka akhoza kuombola. Ndipo akapanda kuiombola kufikira kutha kwake kwa chaka champhumphu, nyumba ili m'mudzi wa m'lingayi idzakhala yake ya iye adaigula yosamchokeranso mwa mibadwo yake; siidzatuluka chaka choliza lipenga. Koma nyumba za m'midzi yopanda linga aziyese monga minda ya m'dziko; ziomboledwe, zituluke m'chaka choliza lipenga. Kunena za midzi ya Alevi, nyumba za m'midzi yaoyao, Alevi akhoza kuziombola nthawi zonse. Ndipo munthu akagula kwa Mlevi, nyumba yogulayo yokhala m'mudzi wakewake, ituluke m'chaka choliza lipenga, popeza nyumba za m'midzi ya Alevi ndizo zaozao mwa ana a Israele. Koma dambo la podyera pao siligulika; popeza ndilo laolao kosatha. Ndipo mbale wako akasaukira chuma, ndi dzanja lake lisowa; iwe uzimgwiriziza; akhale nawe monga mlendo wakugonera kwanu. Usamambwezetsa phindu, kapena chionjezero; koma uope Mulungu wako; kuti mbale wako akhale nawe. Musamampatsa ndalama zako polira phindu, kapena kumpatsa zakudya kuti aonjezerepo pochibwezera. Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani m'dziko la Ejipito, kukupatsani dziko la Kanani, kuti ndikhale Mulungu wanu. Ndipo mbale wako akasaukira chuma, ndi kudzigulitsa kwa iwe; usamamgwiritsa ntchito monga kapolo; azikhala nawe ngati wolipidwa ntchito, ngati mlendo wako; akutumikire kufikira chaka choliza lipenga. Pamenepo azituluka kukuchokera, iye ndi ana ake omwe, nabwerere ku mbumba yake; abwerere ku dziko laolao la makolo ake. Pakuti iwo ndiwo atumiki anga, amene ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito; asamawagulitsa monga amagulitsa kapolo. Usamamweruza momzunza; koma uope Mulungu wako. Kunena za kapolo wako wamwamuna, kapena wamkazi amene ukhala nao; azikhala a amitundu akuzungulira inu, kwa iwowa muzigula akapolo aamuna ndi aakazi. Muwagulenso ana a alendo akukhala mwa inu, a iwowa ndi a mabanja ao akukhala nanu, amene anabadwa m'dziko lanu; ndipo adzakhala anuanu. Ndipo muwayese cholowa cha ana anu akudza m'mbuyo, akhale aoao; muwayese akapolo kosatha; koma za abale anu, ana a Israele, musamalamulirana mozunza. Ndipo mlendo wakugonera kwanu akalemera chuma, ndi mbale wako wakukhala naye akasauka, nadzigulitsa kwa mlendo wakugonera kwanu, kapena kwa fuko la banja la mlendo; atatha kudzigulitsa, aomboledwe; wina wa abale ake amuombole; kapena mbale wa atate wake, kapena mwana wa mbale wa atate wake amuombole, kapena mbale wake aliyense wa banja lake amuombole; kapena akalemera chuma yekha adziombole yekha. Ndipo awerengere amene anamgulayo kuyambira chaka adadzigulitsa kwa iye kufikira chaka choliza lipenga; ndipo mtengo wake ukhale monga mwa kuwerenga kwa zaka; amuyesere monga masiku a munthu wolipidwa. Zikamtsalira zaka zambiri, monga mwa izi abwezere ndalama zakumuombola zochokera ku ndalama zomgulazo. Ndipo zikamtsalira zaka pang'ono kufikira chaka choliza lipenga amwerengere; monga mwa zaka zake abwezere mtengo wake wakumuombola. Akhale naye monga wolipidwa chaka ndi chaka; asamamlamulira momzunza pamaso pako. Ndipo akapanda kumuombola motero, azituluka chaka choliza lipenga, iye ndi ana ake omwe. Pakuti ana a Israele ndi atumiki anga; iwo ndiwo atumiki anga amene ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito; Ine ndine Yehova Mulungu wanu. Musamadzipangira mafano, kapena kudziutsira mafano osema, kapena choimiritsa, kapena kuika mwala wozokota m'dziko mwanu kuugwadira umene; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wanu. Musunge masabata anga, ndi kuchitira ulemu malo anga opatulika; Ine ndine Yehova. Mukamayenda m'malemba anga, ndi kusunga malamulo anga, ndi kuwachita; ndidzakupatsani mvula m'nyengo zake, ndi dziko lidzapereka zipatso zake, ndi mitengo ya m'minda idzabala zipatso zake. Ndipo nyengo yopuntha tirigu idzafikira nyengo yotchera mphesa, ndi nyengo yotchera mphesa idzafikira nyengo zobzala; ndipo mudzakhuta nacho chakudya chanu, ndi kukhala m'dziko mwanu okhazikika. Ndipo ndidzapatsa mtendere m'dzikomo, kuti mudzagone pansi, wopanda wina wakukuopsani; ndidzaletsanso zilombo zisakhale m'dzikomo, lupanga lomwe silidzapita m'dziko mwanu. Mudzapirikitsa adani anu, ndipo adzagwa pamaso panu ndi lupanga. Asanu a inu adzapirikitsa zana limodzi, ndi zana limodzi la inu adzapirikitsa zikwi khumi; ndi adani anu adzagwa pamaso panu ndi lupanga. Ndipo ndidzatembenukira kwa inu, ndi kukubalitsani, ndi kukuchulukitsani; ndipo ndidzakhazika chipangano changa ndinapangana nanucho. Ndipo mudzadya za sundwe wakale ndi kutulutsa zakale chifukwa cha zatsopano. Ndidzamanga Kachisi wanga pakati pa inu, ndipo moyo wanga sudzanyansidwa nanu. Ndipo ndidzayendayenda pakati pa inu, ndi kukhala Mulungu wanu ndi inu mudzakhala anthu anga. Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani m'dziko la Ejipito, kuti musakhale akapolo ao; ndipo ndinathyola mitengo ya magoli anu, ndi kukuyendetsani choweramuka. Koma mukapanda kundimvera Ine, osachita malamulo awa onse; ndipo mukakaniza malemba anga, ndi moyo wanu ukanyansidwa nao maweruzo anga, kotero kuti simudzachita malamulo anga onse, koma kuthyola chipangano changa; ndidzachitira inu ichinso; ndidzakuikirani zoopsa, nthenda yoondetsa ya m'chifuwa ndi malungo, zakulanda maso ndi mphamvu, ndi kuzunza moyo; ndipo mudzabzala mbeu zanu chabe, popeza adani anu adzazidya. Ndipo nkhope yanga idzatsutsana nanu; kuti adani anu adzakukanthani, ndipo akudana ndi inu adzachita ufumu pa inu ndipo mudzathawa wopanda wakukulondolani. Ndipo mukapanda kundimvera, zingakhale izi, ndidzaonjeza kukulangani kasanu ndi kawiri chifukwa cha zochimwa zanu. Popeza ndidzathyola mphamvu yanu yodzikuza; ndi kusandutsa thambo lanu likhale ngati chitsulo ndi dziko lanu ngati mkuwa; ndipo mudzachita nayo mphamvu yanu chabe; ndi nthaka yanu siidzapereka zipatso zake, ndi mitengo ya m'dziko siidzabala zobala zake. Ndipo mukayenda motsutsana nane, osalola kumvera Ine; ndidzakuonjezerani miliri kasanu ndi kawiri, monga mwa zochimwa zanu. Popeza ndidzatumiza chilombo cha kuthengo pakati pa inu, ndipo chidzalanda ana anu, ndi kuononga zoweta zanu nichidzachepetsa inu kuti mukhale pang'ono; ndi njira zanu zidzakhala zakufa. Ndipo mukapanda kulangika nazo ndi kubwera kwa Ine, mukayenda motsutsana ndi Ine; Inenso ndidzayenda motsutsana ndi inu; ndipo ndidzakukanthani Inedi kasanu ndi kawiri chifukwa cha zoipa zanu. Ndipo ndidzadzetsa kwa inu lupanga lakuchita chilango cha chipangano; kotero kuti mudzasonkhanidwa m'midzi mwanu; ndipo ndidzatumiza mliri pakati pa inu; ndipo mudzaperekedwa m'manja mwa mdani. Pamene ndithyola mchirikizo wanu wa mkate, akazi khumi adzaphika mkate wanu mu mchembo umodzi, nadzabweza mkate wanu ndi kuuyesa; ndipo mudzadya, koma osakhuta. Ndipo mukapanda kundimvera Ine, chingakhale ichi, ndi kuyenda motsutsana nane; Ine ndidzayenda nanu motsutsana mwa kukuzazirani, ndi kukulangani Inedi kasanu ndi kawiri chifukwa cha zochimwa zanu. Ndipo mudzadya nyama ya ana anu amuna; inde nyama ya ana anu akazi mudzaidya. Ndipo ndidzaononga malo amsanje anu, ndi kulikha zoimiritsa zanu za dzuwa, ndi kuponya mitembo yanu pa mitembo ya mafano anu; ndi moyo wanga udzanyansidwa nanu. Ndipo ndidzasandutsa midzi yanu bwinja, ndi kupasula malo anu opatulika, wosanunkhiza Ine za fungo lanu lokoma. Inde, ndidzapasula dzikoli, ndipo adani anu akukhala m'mwemo adzadabwa nako. Ndipo ndidzabalalitsa inu mwa amitundu, ndi kusolola lupanga kukutsatani; ndi dziko lanu lidzakhala lopasuka, ndi midzi yanu idzakhala bwinja. Pamenepo dzikoli lidzakondwera nao masabata ake, masiku onse a kupasuka kwake, pokhala inu m'dziko la adani anu; pamenepo dziko lidzapumula, ndi kukondwera nao masabata ake. Masiku onse a kupasuka kwake lipumula; ndiko mpumulo udalisowa m'masabata anu, pokhala inu pamenepo. Kunena za iwo akutsalira, ndidzalonga kukomoka kumtima kwao m'maiko a adani ao; ndi liu la tsamba lotengeka ndi mphepo lidzawapirikitsa; ndipo adzathawa monga amathawa lupanga; ndipo adzagwa wopanda wakuwalondola. Ndipo adzakhumudwitsana monga pothawa lupanga, wopanda wakuwalondola; ndipo mudzakhala opanda mphamvu yakuima pamaso pa adani anu. Ndipo mudzatayika mwa amitundu, ndi dziko la adani anu lidzakudyani. Ndipo otsala mwa inu adzazunzika m'moyo ndi mphulupulu zao m'maiko a adani anu; ndiponso ndi mphulupulu za makolo ao adzazunzika m'moyo. Pamenepo adzavomereza mphulupulu zao, ndi mphulupulu za makolo ao, pochita zosakhulupirika pa Ine; ndiponso popeza anayenda motsutsana ndi Ine, Inenso ndinayenda motsutsana nao, ndi kuwatengera ku dziko la adani ao. Ngati tsono mtima wao wosadulidwa udzichepetsa, ndipo avomereza kulanga kwa mphulupulu zao; pamenepo ndidzakumbukira pangano langa ndi Yakobo; ndiponso pangano langa ndi Isaki, ndiponso pangano langa ndi Abrahamu ndidzakumbukira; ndipo ndidzakumbukira dzikoli. Dziko lomwe lidzasiyidwa nao, ndi kukondwera ndi masabata ake, pokhala lopasuka, iwowa palibe; ndipo iwo adzavomereza kulanga kwa mphulupulu zao; popeza, inde popeza anakaniza maweruzo anga, ndi moyo wao unanyansidwa nao malemba anga. Ndiponso pali ichinso: pokhala iwo m'dziko la adani ao sindidzawakaniza, kapena kunyansidwa nao, kuwaononga konse, ndi kuthyola pangano langa ndinapangana nao; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wao. Koma chifukwa cha iwo ndidzawakumbukira pangano la makolo ao, amene ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito pamaso pa amitundu, kuti ndikhale Mulungu wao; Ine ndine Yehova. Awa ndi malemba ndi maweruzo ndi malamulo amene Yehova anaika pakati pa Iye ndi ana a Israele m'phiri la Sinai, ndi dzanja la Mose. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Pamene munthu achita chowinda cha padera, anthuwo azikhala a Yehova monga mwa kuyesa kwako. Ukayesa wamwamuna wa zaka makumi awiri kufikira wina wa zaka makumi asanu ndi limodzi, uziwayesera a masekeli makumi asanu a siliva, monga mwa sekeli wa malo opatulika. Koma akakhala wamkazi, umuyesere wa masekeli makumi atatu. Akakhala munthu wa zaka zisanu kufikira wina wa zaka makumi awiri uwayesere, wamwamuna wa masekeli makumi awiri, ndi wamkazi wa masekeli khumi. Akakhala mwana wa mwezi umodzi kufikira zaka zisanu, uziwayesera wamwamuna wa masekeli asanu a siliva, ndi wamkazi wa masekeli atatu a siliva. Akakhala munthu wa zaka makumi asanu ndi limodzi ndi mphambu, akakhala wamwamuna, umuyesere wa masekeli khumi ndi asanu, akakhala wamkazi wa masekeli khumi. Koma chuma chake chikapanda kufikira kuyesa kwako, amuike pamaso pa wansembe, kuti wansembeyo amuyese; ndipo wansembeyo amuyese, monga akhoza iye amene anawinda. Ndipo chikakhala cha nyama imene anthu amabwera nayo ikhale chopereka cha Yehova, zonse zotere munthu akazipereka kwa Yehova zikhale zopatulika. Asaisinthe, yokoma m'malo mwa yoipa, kapena yoipa m'malo mwa yokoma; ndipo akasinthadi nyama m'malo mwa inzake, pamenepo iyo ndi yosinthikayo zikhale zopatulika. Ndipo chikakhala cha nyama yodetsa, imene sabwera nayo ikhale chopereka cha Yehova, aike nyamayi pamaso pa wansembe; ndipo wansembeyo aiyese mtengo wake, ingakhale yokoma kapena yoipa; monga uiyesa wansembewe, momwemo. Ndipo akaiombola ndithu, pamenepo aonjezepo limodzi la magawo asanu la mtengo wake. Munthu akapatula nyumba yake ikhale yopatulika kwa Yehova, wansembe aziiyesa mtengo wake, ingakhale yokoma kapena yoipa; monga wansembeyo aiyesa, ikhale momwemo. Ndipo iye wakuipatula akaombola nyumba yake, aonjezepo limodzi la magawo asanu la ndalama za kuyesa kwako, ndipo idzakhala yake. Munthu akapatulirako Yehova munda wakewake, uziuyesa monga mwa mbeu zake zikakhala; homeri wa barele uuyese wa masekeli makumi asanu a siliva. Akapatula munda wake kuyambira chaka choliza lipenga, mundawo ukhale monga momwe unauyesera. Akaupatula munda wake chitapita chaka choliza lipenga, wansembe azimwerengera ndalama monga mwa zaka zotsalira kufikira chaka choliza lipenga, nazichepsako pa kuyesa kwako. Ndipo wakupatula mundayo akauomboladi, aonjezeko limodzi la magawo asanu la ndalama za kuyesa kwako, ndipo uzikhalitsa wake. Koma akapanda kuombola mundawo, kapena atagulitsa mundawo kwa munthu wina, suomboledwanso; koma potuluka m'chaka choliza lipenga, mundawo ukhale wopatulikira Yehova, ngati munda woperekedwa chiperekere kwa Mulungu; ukhale wakewake wa wansembe. Ndipo akapatulira Yehova munda woti adaugula, wosati wogawako ku munda wakewake; pamenepo wansembeyo amwerengere mtengo wake wa kuyesa kwako kufikira chaka choliza lipenga; ndipo apereke kuyesa kwako tsiku lomwelo, chikhale chinthu chopatulikira Yehova. Chaka choliza lipenga mundawo ubwerere kwa iye amene adaugulitsa, kwa iye amene dzikoli ndi lakelake. Ndipo kuyesa kwako konse kukhale monga mwa sekeli wa malo opatulika sekeli ndi magera makumi awiri. Komatu woyamba kubadwa mwa nyama akhale wobadwa woyamba wa Yehova, munthu asampatule; ingakhale ng'ombe ingakhale nkhosa, ndiye wa Yehova. Koma akakhala wa nyama zodetsa, azimuombola monga mwa kuyesa kwako, naonjezepo limodzi la magawo asanu la mtengo wake; ndipo akapanda kumuombola, amgulitse monga mwa kuyesa kwako. Koma asachigulitse kapena kuchiombola chinthu choperekedwa chiperekere kwa Mulungu, chimene munthu achipereka chiperekere kwa Yehova, chotengako ku zonse ali nazo, ngakhale munthu, kapena nyama, kapena munda wakewake; chilichonse choperekedwa chiperekere kwa Mulungu nchopatulika kwambiri. Asamuombole munthu woperekedwa chiperekere kwa Mulungu; amuphe ndithu. Limodzi mwa magawo khumi la zonse m'dziko, la mbeu zake za dziko, la zipatso za mtengo, ndilo la Yehova; likhale lopatulikira Yehova. Koma munthu akaombolatu kanthu ka limodzi la magawo khumiwo aonjezeko limodzi la magawo asanu. Ndipo limodzi la magawo khumi lonse la ng'ombe, kapena la nkhosa, kapena la mbuzi, zilizonse zimapita pansi pa ndodo, limodzi la magawo khumi likhala lopatulikira Yehova. Asafunse ngati yabwino kapena yoipa, kapena kuisintha; koma akaisinthatu, pamenepo iyo ndi yosinthikayo zikhale zopatulika zonse ziwiri; asamaiombola. Awa ndi malamulo, amene Yehova anauza Mose, awauze ana a Israele, m'phiri la Sinai. Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'chipululu cha Sinai, m'chihema chokomanako, tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, chaka chachiwiri atatuluka m'dziko la Ejipito, ndi kuti, Werenga khamu lonse la ana a Israele, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba ya makolo ao ndi kuwerenga maina ao, amuna onse mmodzimmodzi. Iwe ndi Aroni muwawerenge monga mwa magulu ao, onse m'Israele akutuluka ku nkhondo, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu. Ndipo pamodzi ndi inu pakhale munthu mmodzi wa mafuko onse; yense mkulu wa nyumba ya kholo lake. Ndipo maina a amuna amene aime nanu ndi awa: wa Rubeni, Elizuri mwana wa Sedeuri. Wa Simeoni, Selumiele mwana wa Zurishadai. Wa Yuda, Nasoni mwana wa Aminadabu. Wa Isakara, Netanele mwana wa Zuwara. Wa Zebuloni, Eliyabu mwana wa Heloni. Wa ana a Yosefe: wa Efuremu, Elisama mwana wa Amihudi; wa Manase, Gamaliele mwana wa Pedazuri. Wa Benjamini, Abidani mwana wa Gideoni. Wa Dani, Ahiyezere mwana wa Amisadai. Wa Asere, Pagiyele mwana wa Okarani. Wa Gadi, Eliyasafu mwana wa Deuwele. Wa Nafutali, Ahira mwana wa Enani. Iwo ndiwo oitanidwa a khamu, akalonga a mafuko a makolo ao; ndiwo akulu a zikwizo za Israele. Ndipo Mose ndi Aroni anatenga anthu awa, onenedwa maina ao; nasonkhanitsa khamu lonse tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, ndipo iwo anawakumbira magwero ao kutchula mabanja ao, ndi nyumba za makolo ao, ndi kuwerenga maina kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu mmodzimmodzi. Monga Yehova anauza Mose, momwemo anawawerenga m'chipululu cha Sinai. Ndipo ana a Rubeni, mwana woyamba wa Israele, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina mmodzimmodzi, amuna onse kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo; owerengedwa ao a fuko la Rubeni, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu ndi chimodzi kudza mazana asanu. A ana a Simeoni, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, owerengedwa ao, powerenga maina mmodzimmodzi, amuna onse kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo; owerengedwa ao a fuko la Simeoni, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi zinai kudza mazana atatu. A ana a Gadi, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo; owerengedwa ao a fuko la Gadi, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu. A ana a Yuda, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo; owerengedwa ao a fuko la Yuda, ndiwo zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zinai kudza mazana asanu ndi limodzi. A ana a Isakara, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo; owerengedwa ao a fuko la Isakara, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zinai kudza mazana anai. A ana a Zebuloni, kubadwa kwao, monga nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo; owerengedwa ao a fuko la Zebuloni, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi ziwiri kudza mazana anai. A ana a Yosefe, ndiwo a ana a Efuremu, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo; owerengedwa ao a fuko la Efuremu, ndiwo zikwi makumi anai mphambu mazana asanu. A ana a Manase, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo; owerengedwa ao a fuko la Manase, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu ziwiri kudza mazana awiri. A ana a Benjamini, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo; owerengedwa ao a fuko la Benjamini, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu zisanu kudza mazana anai. A ana a Dani, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo; owerengedwa ao a fuko la Dani, ndiwo zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi awiri. A ana a Asere, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo; owerengedwa ao a fuko la Asere, ndiwo zikwi makumi anai mphambu chimodzi kudza mazana asanu. A ana a Nafutali, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo; owerengedwa ao a fuko la Nafutali, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zitatu kudza mazana anai. Iwo ndiwo amene anawerengedwa, amene Mose anawerenga pamodzi ndi Aroni, ndi akalonga a Israele, ndiwo amuna khumi ndi awiri; yense kunenera nyumba ya kholo lake. Potero owerengedwa onse a ana a Israele monga mwa nyumba za makolo ao, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo m'Israele; inde owerengedwa onse ndiwo zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi makumi asanu. Koma Alevi monga mwa fuko la makolo ao sanawerengedwe mwa iwo. Popeza Yehova adalankhula ndi Mose, ndi kuti, Fuko la Levi lokha usaliwerenge, kapena kuona kufikira kwao mwa ana a Israele; koma iwe, uike Alevi asunge Kachisi wa mboni, ndi zipangizo zake zonse, ndi zonse ali nazo; azinyamula Kachisi, ndi zipangizo zake zonse; namtumikire, namange mahema ao pozungulira pa Kachisi. Ndipo akati amuke naye Kachisiyo, Alevi amgwetse, ndipo akati ammange, Alevi amuimike; ndipo mlendo akayandikizako amuphe. Ndipo ana a Israele amange mahema ao, yense ku chigono chake, ndi yense ku mbendera yake, monga mwa makamu ao. Koma Alevi amange mahema ao pozungulira pa Kachisi wa mboni, kuti mkwiyo ungagwere khamu la ana a Israele; ndipo Alevi azidikira Kachisi wa mboni. Momwemo ana a Israele anachita monga mwa zonse Yehova adauza Mose; anachita momwemo. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati, Ana a Israele azimanga mahema ao yense ku mbendera yake, ya chizindikiro cha nyumba ya kholo lake; amange mahema ao popenyana ndi chihema chokomanako pozungulira. Ndipo iwo akumanga mahema ao ku m'mawa kotuluka dzuwa ndiwo a mbendera ya chigono cha Yuda, monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana Yuda ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu. Ndipo khamu lake, ndi owerengedwa ao, ndiwo zikwi makumi asanu ndi awiri, mphambu zinai, kudza mazana asanu ndi limodzi. Ndipo iwo akumanga mahema ao poyandikizana naye ndiwo a fuko la Isakara; ndipo kalonga wa ana a Isakara ndiye Netanele mwana wa Zuwara. Ndipo khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zinai kudza mazana anai. Ndi fuko la Zebuloni: kalonga wa ana a Zebuloni ndiye Eliyabu mwana wa Heloni. Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi ziwiri kudza mazana anai. Owerengedwa onse a chigono cha Yuda ndiwo zikwi makumi khumi mphambu makumi asanu ndi atatu kudza zisanu ndi chimodzi mphambu mazana anai, monga mwa makamu ao. Ndiwo azitsogolera ulendo. Mbendera ya chigono cha Rubeni ikhale kumwera monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana a Rubeni ndiye Elizuri mwana wa Sedeuri. Ndi khamu lake, ndi olembedwa ake, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu ndi chimodzi kudza mazana asanu. Ndipo iwo akumanga mahema ao poyandikizana naye ndiwo a fuko la Simeoni; ndi kalonga wa ana a Simeoni ndiye Selumiele mwana wa Zurishadai. Ndi khamu lake ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi zinai kudza mazana atatu. Ndi fuko la Gadi; kalonga wa ana a Gadi ndiye Eliyasafu mwana wa Reuwele. Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu. Owerengedwa onse a chigono cha Rubeni ndiwo zikwi makumi khumi mphambu makumi asanu ndi chimodzi kudza mazana anai mphambu makumi asanu, monga mwa makamu ao. Ndiwo azitsatana nao otsogolerawo. Pamenepo khamu la Alevi azimuka nacho chihema chokomanako, pakati pa makamu; monga amamanga mahema ao, momwemo azimuka ulendo wao, munthu yense pamalo pake, monga mwa mbendera zao. Mbendera ya chigono cha Efuremu izikhala kumadzulo monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana a Efuremu ndiye Elisama mwana wa Amihudi. Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi anai kudza mazana asanu. Ndipo oyandikizana naye ndiwo a fuko la Manase; ndi kalonga wa ana a Manase ndiye Gamaliele mwana wa Pedazuri. Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu ziwiri kudza mazana awiri. Ndi fuko la Benjamini: kalonga wa ana a Benjamini ndiye Abidani mwana wa Gideoni. Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu zisanu kudza mazana anai. Owerengedwa onse a chigono cha Efuremu ndiwo zikwi makumi khumi mphambu zisanu ndi zitatu kudza zana limodzi, monga mwa makamu ao. Iwo ndiwo aziyenda gulu lachitatu paulendo. Mbendera ya chigono cha Dani izikhala kumpoto monga mwa makamu ao; ndi kalonga wa ana a Dani ndiye Ahiyezere mwana wa Amisadai. Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi awiri. Ndipo iwo a kumanga mahema ao poyandikizana naye ndiwo a fuko la Asere; ndi kalonga wa ana a Asere ndiye Pagiyele mwana wa Okarani. Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi anai mphambu chimodzi kudza mazana asanu. Ndi fuko la Nafutali: ndi kalonga wa ana a Nafutali ndiye Ahira mwana wa Enani. Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zitatu kudza mazana anai. Owerengedwa onse a chigono cha Dani ndiwo zikwi makumi khumi mphambu makumi asanu kudza zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu ndi limodzi. Iwo ndiwo aziyenda m'mbuyo paulendo, monga mwa mbendera zao. Amenewo ndiwo anawerengedwa a ana a Israele monga mwa nyumba za makolo ao; owerengedwa onse a m'zigono, monga mwa makamu ao, ndiwo zikwi makumi khumi kasanu ndi kamodzi mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi makumi asanu. Koma sanawerenge Alevi mwa ana a Israele; monga Yehova adauza Mose. Ndipo ana a Israele anachita monga mwa zonse Yehova adauza Mose, momwemo anamanga mahema ao pa mbendera zao, momwemonso anayenda paulendo, yense monga mwa mabanja ake, monga mwa nyumba za makolo ake. Mibadwo ya Aroni ndi Mose, tsiku lija Yehova ananena ndi Mose m'phiri la Sinai, ndi iyo. Ndipo maina ao a ana amuna a Aroni ndi awa: Woyamba Nadabu, ndi Abihu, Eleazara, ndi Itamara. Awa ndi maina a ana amuna a Aroni, ansembe odzozedwawo, amene anawadzaza manja ao achite ntchito ya nsembe. Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamaso pa Yehova muja anabwera nao moto wachilendo pamaso pa Yehova, m'chipululu cha Sinai, ndipo analibe ana; koma Eleazara ndi Itamara anachita ntchito ya nsembe pamaso pa atate wao Aroni. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Sendera nalo kuno fuko la Levi, ndi kuwaika pamaso pa Aroni wansembe, kuti amtumikire. Ndipo azisunga udikiro wake, ndi udikiro wa khamu lonse pa khomo la chihema chokomanako, kuchita ntchito ya Kachisi. Ndipo asunge zipangizo zonse za chihema chokomanako, ndi udikiro wa ana a Israele, kuichita ntchito ya Kachisi. Ndipo uzipereka Alevi kwa Aroni ndi kwa ana ake amuna; apatsidwa kwa iye ndithu, ochokera kwa ana a Israele. Koma uike Aroni ndi ana ake amuna, azisunga ntchito yao ya nsembe; ndi mlendo wakusendera pafupi amuphe. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Ndipo taonani, Ine ndatenga Alevi kuwachotsa pakati pa ana a Israele m'malo mwa ana oyamba onse, oyamba kubadwa mwa ana a Israele; ndipo Aleviwo ndi anga. Pakuti ana oyamba onse ndi anga; tsiku lija ndinakantha ana oyamba onse m'dziko la Ejipito ndinadzipatulira ana oyamba onse m'Israele, kuyambira munthu kufikira choweta; ndiwo anga; Ine ndine Yehova. Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'chipululu cha Sinai, nati Werenga ana a Levi monga mwa nyumba ya makolo ao, monga mwa mabanja ao; uwawerenge mwamuna yense wa mwezi umodzi ndi mphambu. Ndipo Mose anawawerenga monga mwa mau a Yehova, monga adamuuza. Ndipo ana a Levi maina ao ndi awa: Geresoni, ndi Kohati ndi Merari. Ndi ana a Geresoni maina ao ndi awa, monga mwa mabanja ao: Libini, ndi Simei. Ndi ana a Kohati monga mwa mabanja ao: Amuramu ndi Izihara, Hebroni ndi Uziyele. Ndi ana a Merari monga mwa mabanja ao: Mali ndi Musi. Awa ndi mabanja a Alevi monga mwa nyumba za makolo ao. Banja la Libini, ndi mabanja a Simei, ndiwo a Geresoni; ndiwo mabanja a Geresoni. Owerengedwa ao, powawerenga amuna onse, kuyambira mwana wa mwezi umodzi ndi mphambu, owerengedwa ao ndiwo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu. Mabanja a Ageresoni azimanga mahema ao pambuyo pa Kachisi kumadzulo. Ndipo kalonga wa nyumba ya makolo a Ageresoni ndiye Eliyasafu mwana wa Laele. Ndipo udikiro wa ana a Geresoni m'chihema, chokomanako ndiwo Kachisi, ndi chihema, chophimba chake, ndi nsalu yotsekera pa khomo la chihema chokomanako, ndi nsalu zotchinga za kubwalo, ndi nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo, lokhala ku Kachisi, ndi ku guwa la nsembe pozungulira, ndi zingwe zake za ku ntchito zake zonse. Banja la Aamuramu, ndi banja la Aizihara, ndi banja la Ahebroni, ndi banja la Auziyele ndiwo a Kohati; ndiwo mabanja a Akohati. Powawerenga amuna onse, kuyambira a mwezi umodzi ndi mphambu ndiwo zikwi zisanu ndi zitatu mphambu mazana asanu ndi limodzi, akusunga udikiro wa pa malo opatulika. Mabanja a ana a Kohati azimanga mahema ao pa mbali ya Kachisi ya kumwera. Ndipo kalonga wa nyumba ya makolo ao ya mabanja a Akohati ndiye Elizafani mwana wa Uziyele. Ndipo udikiro wao ndiwo likasa, ndi gome, ndi choikapo nyali, ndi magome a nsembe, ndi zipangizo za malo opatulika zimene achita nazo, ndi nsalu yotchinga, ndi ntchito zake zonse. Ndipo kalonga wa akalonga a Alevi ndiye Eleazara mwana wa Aroni wansembeyo; ndiye aziyang'anira osunga udikiro wa pa malo opatulika. Banja la Amali, ndi banja la Amusi ndiwo a Merari; ndiwo mabanja a Merari. Ndipo owerengedwa ao, powerenga amuna onse, kuyambira a mwezi umodzi ndi mphambu, ndiwo zikwi zisanu ndi chimodzi kudza mazana awiri. Ndi kalonga wa nyumba ya makolo ya mabanja la Merari ndiye Zuriyele mwana wa Abihaili; azimanga mahema ao pa mbali ya Kachisi ya kumpoto. Ndipo choyang'anira iwo, udikiro wao wa ana a Merari ndiwo matabwa a Kachisi, ndi mitanda yake, ndi mizati ndi nsanamira zake, ndi makamwa ake, ndi zipangizo zake zonse, ndi ntchito zake zonse; ndi nsichi za pabwalo pozungulira, ndi makamwa ake, ndi zichiri zake, ndi zingwe zake. Ndipo amene adamanga mahema ao pa khomo la Kachisi, kum'mawa, pa khomo la chihema chokomanako kotulukira dzuwa, ndiwo Mose ndi Aroni, ndi ana ake amuna, akusunga udikiro wa malo opatulika, ndiwo udikiro wa ana a Israele; koma mlendo wakuyandikizako amuphe. Owerengedwa onse a Alevi, adawawerenga Mose ndi Aroni, powauza Yehova, monga mwa mabanja ao, amuna mphambu, ndiwo zikwi makumi awiri mphambu ziwiri. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Werenga amuna oyamba kubadwa onse a ana a Israele kuyambira a mwezi umodzi ndi mphambu nuone chiwerengo cha maina ao. Ndipo unditengere Ine Alevi (Ine ndine Yehova) m'malo mwa oyamba kubadwa onse mwa ana a Israele; ndi ng'ombe za Alevi m'malo mwa zoyamba kubadwa zonse mwa ng'ombe za ana a Israele. Ndipo Mose anawawerenga, monga Yehova adamuuza, oyamba kubadwa onse mwa ana a Israele. Ndipo amuna onse oyamba kubadwa, powerenga maina, kuyambira a mwezi umodzi ndi mphambu, owerengedwa ao, ndiwo zikwi makumi awiri mphambu ziwiri kudza mazana awiri ndi makumi asanu ndi awiri mphambu atatu. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Landira Alevi m'malo mwa oyamba kubadwa onse mwa ana a Israele, ndi ng'ombe za Alevi m'malo mwa ng'ombe zao; ndipo Alevi azikhala anga; Ine ndine Yehova. Kunena za mazana awiri ndi makumi asanu ndi awiri kudza atatuwo oyamba kubadwa a ana a Israele, akuposa Alevi, akaomboledwe, ulandire masekeli asanu pa munthu mmodzi; uwalandire pa muyeso wa sekeli wa malo opatulika (sekeli ndiwo magera makumi awiri); nupereke ndalama zimene akuposawo anaomboledwa nazo kwa Aroni ndi kwa ana ake amuna. Pamenepo Mose analandira ndalama zoombola nazo kwa iwo akuposa aja adawaombola Alevi; analandira ndalamazo kwa oyamba kubadwa a ana a Israele; masekeli chikwi chimodzi mphambu mazana atatu kudza makumi asanu ndi limodzi mphambu asanu, kuyesa sekeli wa malo opatulika. Ndipo Mose anapatsa Aroni ndi ana ake ndalama zoombola nazo monga mwa mau a Yehova, monga Yehova adauza Mose. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati, Werengani ana a Kohati pakati pa ana a Levi, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu, kufikira zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu, kuti agwire ntchito ya chihema chokomanako. Ntchito ya ana a Kohati m'chihema chokomanako ndi iyi, kunena za zinthu zopatulika kwambiri: akati amuke a m'chigono, Aroni ndi ana ake amuna azilowa, natsitse nsalu yotchinga, ndi kuphimba nayo likasa la mboni, ndi kuikapo chophimba cha zikopa za akatumbu; ndi kuyalapo nsalu yamadzi yeniyeni, ndi kupisako mphiko zake. Ndi pa gome la mkate woonekera ayale nsalu yamadzi, naikepo mbale zake, ndi zipande, ndi mitsuko, ndi zikho zakuthira nazo; mkate wa chikhalire uzikhalaponso. Ndipo ayale pa izi nsalu yofiira, ndi kuliphimba ndi chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zake. Ndipo atenge nsalu yamadzi, ndi kuphimba choikapo nyali younikira, ndi nyali zake, ndi mbano zake, ndi zoolera zake, ndi zotengera zake zonse za mafuta zogwira nazo ntchito yake. Ndipo achimange ndi chipangizo zake zonse m'chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kuziika pa chonyamulira. Ndipo pa guwa la nsembe lagolide aziyala nsalu ya madzi, naliphimbe ndi chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zake. Natenge zipangizo zake zonse za utumiki, zimene atumikira nazo m'malo opatulika, nazimange m'nsalu yamadzi, ndi kuziphimba ndi chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kuziika pachonyamulira. Ndipo azichotsa mapulusa pa guwa la nsembe, ndi kuyala pa ilo nsalu yofiirira. Naikepo zipangizo zake zonse, zimene atumikira nazo pamenepo, mbale za zofukiza, mitungo, ndi zoolera, ndi mbale zowazira, zipangizo zonse za guwa la nsembe; nayalepo chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kupisako mphiko zake. Atatha Aroni ndi ana ake amuna kuphimba malo opatulika, ndi zipangizo zake zonse za malo opatulika, pofuna kumuka am'chigono; atatero, ana a Kohati adze kuzinyamula; koma asakhudze zopatulikazo, kuti angafe. Zinthu izi ndizo akatundu a ana a Kohati adze m'chihema chokomanako. Ndipo zoyang'anira Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, ndizo mafuta a nyaliyo, ndi chofukiza cha fungo lokoma, ndi nsembe yaufa kosalekeza, ndi mafuta odzoza, udikiro wa Kachisi opatulika, ndi zipangizo zake. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati, Musamasadza fuko la mabanja a Kohati kuwachotsa pakati pa Alevi; koma muzitero nao kuti akhale ndi moyo, osafa ai, poyandikiza iwo zopatulika kwambirizo; Aroni ndi ana ake amuna alowe, namuikire munthu yense ntchito yake ndi katundu wake. Koma asalowe kukaona zopatulikazo pozikulunga, kuti angafe. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Werenganso ana a Geresoni, monga mwa nyumba za makolo ao, monga mwa mabanja ao. Uwawerenge kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu, kufikira a zaka makumi asanu; onse akulowa kutumikira utumikiwo, kuchita ntchitoyi m'chihema chokomanako. Ntchito ya mabanja a Ageresoni, pogwira ntchito ndi kusenza katundu ndi iyi; azinyamula nsalu zophimba za Kachisi, ndi chihema chokomanako, chophimba chake, ndi chophimba cha zikopa za akatumbu chili pamwamba pake, ndi nsalu yotsekera pa khomo la chihema chokomanako; ndi nsalu zochingira za pabwalo, ndi nsalu yotsekera ku chipata cha pabwalo lili pa Kachisi ndi pa guwa la nsembe pozungulira, ndi zingwe zao, ndi zipangizo zonse za ntchito zao, ndi zonse achita nazo; m'menemo muli ntchito zao. Ntchito yonse ya ana a Ageresoni, kunena za akatundu ao ndi ntchito zao zonse, ikhale monga adzanena Aroni ndi ana ake amuna; ndipo muwaike adikire akatundu ao onse. Iyi ndi ntchito ya mabanja a ana a Geresoni m'chihema chokomanako; ndipo Itamara mwana wa Aroni wansembe ayang'anire udikiro wao. Kunena za ana a Merari, Uwawerenge monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao. Uwawerenge kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu, kuchita ntchito ya chihema chokomanako. Ndipo udikiro wa akatundu ao, monga mwa ntchito zao zonse m'chihema chokomanako ndi ichi: matabwa a Kachisi, ndi mitanda yake, ndi mizati ndi nsanamira zake, ndi makamwa ake; ndi nsichi za kubwalo kozungulira, ndi makamwa ake, ndi zichiri zake, ndi zingwe zake, pamodzi ndi zipangizo zake zonse, ndi ntchito yake yonse; ndipo muziwerenga zipangizo za udikiro wa akatundu ao ndi kuwatchula maina ao. Iyi ndi ntchito ya mabanja a ana a Merari, monga mwa ntchito zao zonse m'chihema chokomanako, mowauza Itamara mwana wa Aroni wansembe. Ndipo Mose ndi Aroni ndi akalonga a khamu anawerenga ana a Akohati monga mwa mabanja ao, ndi monga mwa nyumba za makolo ao, kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu, kuti agwire ntchito m'chihema chokomanako; ndipo owerengedwa ao monga mwa mabanja ao ndiwo zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu. Awa ndi owerengedwa a mabanja a Akohati, onse akutumikira m'chihema chokomanako, amene Mose ndi Aroni anawawerenga monga mwa mau a Yehova mwa dzanja la Mose. Ndipo ana owerengedwa a Geresoni, monga mwa mabanja ao, ndi monga mwa nyumba za makolo ao, kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu, kuti agwire ntchito m'chihema chokomanako, owerengedwa ao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, ndiwo zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi limodzi kudza makumi atatu. Amenewo ndiwo owerengedwa a mabanja a ana a Geresoni, onse akutumikira m'chihema chokomanako, adawawerenga Mose ndi Aroni monga mwa mau a Yehova. Ndipo owerengedwa a mabanja a ana a Merari, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu kuti agwire ntchito m'chihema chokomanako, owerengedwa ao monga mwa mabanja ao, ndiwo zikwi zitatu ndi mazana awiri. Amenewo ndiwo owerengedwa a mabanja a ana a Merari, amene Mose ndi Aroni anawawerenga monga mwa mau a Yehova mwa dzanja la Mose. Owerengedwa onse a Alevi, amene Mose ndi Aroni ndi akalonga a Israele anawawerengera, monga mwa mabanja ao, ndi monga mwa nyumba za makolo ao, kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa kugwira ntchito ya utumikiwu, ndiyo ntchito ya akatundu m'chihema chokomanako; owerengedwawo ndiwo zikwi zisanu ndi zitatu kudza mazana asanu mphambu makumi asanu ndi atatu. Anawawerenga monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose, onse monga mwa ntchito zao, ndi monga mwa akatundu ao; anawawerenga monga momwe Yehova adauza Mose. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Uza ana a Israele kuti azitulutsa m'chigono akhate onse, ndi onse akukhala nako kukha, ndi odetsedwa chifukwa cha akufa; muwatulutse amuna ndi akazi muwatulutsire kunja kwa chigono, kuti angadetse chigono chao, chimene ndikhala m'kati mwakemo. Ndipo ana a Israele anachita chotero, nawatulutsira kunja kwa chigono; monga Yehova adanena ndi Mose momwemo ana a Israele anachita. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Nena ndi ana a Israele, ndi kuti Mwamuna kapena mkazi akachita tchimo lililonse amachita anthu, kuchita mosakhulupirika pa Yehova, nakapalamuladi; azivomereza tchimo lake adalichita; nabwezere chopalamulacho monsemo, naonjezeko limodzi la magawo asanu, ndi kuchipereka kwa iye adampalamulayo. Koma munthuyo akapanda kukhala nayo nkhoswe imene akaibwezere chopalamulacho, chopalamula achibwezera Yehovacho chikhale cha wansembe; pamodzi ndi nkhosa yamphongo ya chotetezerapo, imene amchitire nayo chomtetezera. Ndipo nsembe zokweza zonse za zinthu zopatulika za ana a Israele, zimene abwera nazo kwa wansembe zisanduka zake. Zopatulika za munthu aliyense ndi zake: zilizonse munthu aliyense akapatsa wansembe, zasanduka zake. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mkazi wa mwini akapatukira mwamuna wake, nakamchitira mosakhulupirika, ndi munthu akagona naye, koma kumbisikira maso a mwamuna wake, ndi kumng'unira; nadetsedwa mkaziyo, koma palibe mboni yomtsutsa, kapena sanamgwire alimkuchita; ndipo ukamgwira mwamuna mtima wansanje, kuti achitire nsanje mkazi wake, popeza wadetsedwa; kapena ukamgwira mtima wansanje, kuti amchitire mkazi wake nsanje angakhale sanadetsedwe; pamenepo mwamunayo azidza naye mkazi wake kwa wansembe, nadze nacho chopereka chake, limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wabarele; asathirepo mafuta, kapena kuikapo lubani; popeza ndiyo nsembe yaufa yansanje, nsembe yaufa yachikumbutso, yakukumbutsa mphulupulu. Ndipo wansembe abwere naye, namuike pamaso pa Yehova; natenge madzi opatulika m'mbale yadothi wansembeyo, natengeko fumbi lili pansi m'Kachisi, wansembeyo nalithire m'madzimo. Pamenepo wansembeyo aike mkaziyo pamaso pa Yehova, navula mutu wa mkaziyo, naike nsembe yaufa yachikumbutso m'manja mwake, ndiyo nsembe yaufa yansanje; ndipo m'manja mwake mwa wansembe muzikhala madzi owawa akudzetsa temberero. Ndipo wansembe amlumbiritse, nanene kwa mkazi, Ngati sanagone nawe munthu mmodzi yense, ngati sunapatukira kuchidetso, pokhala ndiwe wa mwamuna wako, upulumuke ku madzi owawa awa akudzetsa temberero. Koma iwe, ngati wapatukira mwamuna wako, ngati wadetsedwa, kuti wagona nawe munthu, wosati mwamuna wako; pamenepo wansembe alumbiritse mkazi lumbiro lakutemberera, ndi wansembe anene kwa mkazi, Yehova akuike ukhale temberero ndi lumbiro pakati pa anthu a mtundu wako, pakuondetsa Yehova m'chuuno mwako, ndi kukutupitsa thupi lako; ndipo madzi awa akudzetsa temberero adzalowa m'matumbo mwako, nadzakutupitsa thupi lako ndi kuondetsa m'chuuno mwako; ndipo mkaziyo aziti, Amen, Amen. Ndipo wansembe alembere matemberero awa m'buku, ndi kuwafafaniza ndi madzi owawawa. Ndipo amwetse mkaziyo madzi owawa akudzetsa temberero; ndi madzi odzetsa temberero adzalowa mwa iye nadzamwawira. Ndipo wansembe atenge nsembe yaufa yansanje m'manja mwa mkazi, naweyule nsembe yaufa pamaso pa Yehova, nabwere nayo ku guwa la nsembe. Wansembe atengekonso nsembe yaufa wodzala manja, chikumbutso chake, nachitenthe pa guwa la nsembe; ndipo atatero amwetse mkazi madziwo. Ndipo atammwetsa madziwo, kudzatero, ngati wadetsedwa, nachita mosakhulupirika pa mwamuna wake, madzi odzetsa tembererowo adzalowa mwa iye nadzamwawira, nadzamtupitsa thupi lake, ndi m'chuuno mwake mudzaonda; ndi mkaziyo adzakhala temberero pakati pa anthu a mtundu wake. Koma ngati mkazi sanadetsedwe, nakhala woyera, pamenepo adzapulumuka, nadzaima. Ichi ndi chilamulo cha nsanje, pamene mkazi, pokhala naye mwamuna wake, ampatukira nadetsedwa; kapena pamene mtima wansanje umgwira mwamuna, ndipo achitira mkazi wake nsanje; pamenepo aziika mkazi pamaso pa Yehova, ndipo wansembe amchitire chilamulo ichi chonse. Mwamunayo ndiye wosachita mphulupulu, koma mkazi uyo asenze mphulupulu yake. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mwamuna kapena mkazi akadzipatulira kulonjeza chowinda cha Mnaziri, kudzipatulira kwa Yehova; azisala vinyo ndi kachasu; asamwe vinyo wosasa, kapena kachasu wosasa, kapena chakumwa chonse cha mphesa, asamwe; asadye mphesa zaziwisi kapena zouma. Masiku onse a kusala kwake asadye kanthu kopangika ndi mphesa, kuyambira nthanga zake kufikira khungu lake. Masiku onse a chowinda chake chakusala, lumo lisapite pamutu pake; kufikira adatha masikuwo adadzipatulira kwa Yehova, azikhala wopatulika; aleke nzera za tsitsi lake zimeretu. Masiku onse akudzipatulira kwa Yehova asayandikize mtembo. Asadzidetse ndi atate wake, kapena mai wake, mbale wake, kapena mlongo wake, akafa iwowa; popeza chowindira Mulungu wake chili pamutu pake. Masiku onse a kusala kwake akhala wopatulikira kwa Yehova. Munthu akafa chikomo pali iye, ndipo akadetsa mutu wake wowinda; pamenepo azimeta mutu wake tsiku la kumyeretsa kwake, tsiku lachisanu ndi chiwiri aumete. Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu adze nazo njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, kwa wansembe; ndipo wansembe akonze imodzi nsembe yauchimo, ndi ina nsembe yopsereza, namtetezere popeza anachimwa nao mtembowo; ndipo apatulire mutu wake tsiku lomwelo. Ndipo awapatulire Yehova masiku a kusala kwake, nadze nayo nkhosa yamphongo ya chaka chimodzi ikhale nsembe yopalamula; koma masiku adapitawa azikhala chabe, popeza anadetsa kusala kwake. Ndipo chilamulo cha Mnaziri, atatha masiku a kusala kwake ndi ichi: azidza naye ku khomo la chihema chokomanako; pamenepo abwere nacho chopereka chake kwa Yehova, nkhosa yamphongo ya chaka chimodzi yopanda chilema, ikhale nsembe yopsereza, ndi nkhosa yaikazi yopanda chilema ikhale nsembe yauchimo, ndi nkhosa yamphongo yopanda chilema ikhale nsembe yoyamika; ndi dengu la mkate wopanda chotupitsa, timitanda ta ufa wosalala tosanganiza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi todzoza ndi mafuta, ndi nsembe yao yaufa, ndi nsembe zao zothira. Ndipo wansembe azibwera nazo pamaso pa Yehova, nakonze nsembe yake yauchimo, ndi nsembe yake yopsereza; naphe nkhosa yamphongo yoyamika ya Yehova, pamodzi ndi dengu la mkate wopanda chotupitsa; wansembe akonzenso nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira. Pamenepo Mnaziriyo amete mutu wake wa kusala kwake pa khomo la chihema chokomanako, natenge tsitsi la pa mutu wake wa kusala, naliike pamoto wokhala pansi pa nsembe yoyamika. Ndipo wansembe atenge mwendo wamwamba wophika wa nkhosa yamphongo, ndi kamtanda kamodzi kopanda chotupitsa ka m'dengu, ndi kamtanda kaphanthi kopanda chotupitsa kamodzi, ndi kuziika m'manja mwa Mnaziri, atameta kusala kwake; ndipo wansembe aziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ichi nchopatulikira wansembe, pamodzi ndi nganga ya nsembe yoweyula, pamodzi ndi mwendo wa nsembe yokweza; ndipo atatero Mnaziri amwe vinyo. Ichi ndi chilamulo cha Mnaziri wakuwinda, ndi cha chopereka chake cha Yehova chifukwa cha kusala kwake, pamodzi nacho chimene dzanja lake likachipeza; azichita monga mwa chowinda chake anachiwinda, mwa chilamulo cha kusala. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Nena ndi Aroni ndi ana ake, ndi kuti, Uzidalitsa ana a Israele motero; uziti nao, Yehova akudalitse iwe, nakusunge; Yehova awalitse nkhope yake pa iwe, nakuchitire chisomo; Yehova akweze nkhope yake pa iwe, nakupatse mtendere. Potero aike dzina langa pa ana a Israele; ndipo ndidzawadalitsa. Ndipo kunali kuti tsiku lomwe Mose anatsiriza kumuutsa Kachisi, namdzoza ndi kumpatula, ndi zipangizo zake zonse, ndi guwa la nsembe, ndi zipangizo zake zonse, nazidzoza ndi kuzipatula; akalonga a Israele, akulu a nyumba za makolo ao, anapereka nsembe, ndiwo akalonga a mafuko akuyang'anira owerengedwa; anadza nacho chopereka chao pamaso pa Yehova, magaleta ophimbika asanu ndi mmodzi, ndi kalonga mmodzi ng'ombe imodzi; nabwera nazo pakhomo pa Kachisi. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Uzilandira kwa iwo, kuti zikhale zakuchitira ntchito ya chihema chokomanako; nuzipereke kwa Alevi, yense monga mwa ntchito yake. Ndipo Mose analandira magaleta ndi ng'ombe, nazipereka kwa Alevi. Anapatsa ana a Geresoni magaleta awiri ndi ng'ombe zinai, monga mwa ntchito yao; napatsa ana a Merari magaleta anai ndi ng'ombe zisanu ndi zitatu, monga mwa ntchito yao; wakuziyang'anira ndiye Itamara mwana wa Aroni wansembe. Koma sanapatse ana a Kohati kanthu; popeza ntchito yao ndiyo ya zinthu zopatulika, zimene amazisenza pa mapewa ao. Ndipo akalonga anabwera nazo za kupereka chiperekere guwa la nsembe tsiku lodzozedwa ili; inde akalongawo anabwera nacho chopereka chao pa guwa la nsembelo. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Akalonga onse, yense pa tsiku lake, apereke zopereka zao za kupereka chiperekere guwa la nsembe. Wakubwera nacho chopereka chake tsiku loyamba ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu, wa fuko la Yuda: chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake ndiko masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwirizo zodzala ndi ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta ukhale nsembe yaufa; chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza; ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza; tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Nasoni mwana wa Aminadabu. Tsiku lachiwiri Netanele mwana wa Zuwara, kalonga wa Isakara, anabwera nacho chake: anabwera nacho chopereka chake mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa; chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza; ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza; tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Netanele mwana wa Zuwara. Tsiku lachitatu kalonga wa ana a Zebuloni, ndiye Eliyabu mwana wa Heloni: chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzaza ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa; chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza; ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza; tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Eliyabu mwana wa Heloni. Tsiku lachinai Elizuri, mwana wa Sedeuri, kalonga wa ana a Rubeni: chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika, zonse ziwiri zodzaza ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa; chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza; ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza; tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Elizuri mwana wa Sedeuri. Tsiku lachisanu kalonga wa ana a Simeoni, ndiye Selumiele, mwana wa Zurishadai: chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa; chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza; ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza; tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Selumiele mwana wa Zurishadai. Tsiku lachisanu ndi chimodzi kalonga wa ana a Gadi, Eliyasafu mwana wa Deuwele: chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu; mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa; chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza; ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza; tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Eliyasafu mwana wa Deuwele. Tsiku lachisanu ndi chiwiri kalonga wa ana a Efuremu Elisama mwana wa Amihudi: chopereka chake mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa; chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza; ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza; tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa za mphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Elisama mwana wa Amihudi. Tsiku lachisanu ndi chitatu kalonga wa ana a Manase ndiye Gamaliele mwana wa Pedazuri: chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa; chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza; ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza; tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Gamaliele mwana wa Pedazuri. Tsiku lachisanu ndi chinai kalonga wa ana a Benjamini, ndiye Abidani mwana wa Gideoni: chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa; chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza; ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza; tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Abidani mwana wa Gideoni. Tsiku lakhumi kalonga wa ana a Dani, ndiye Ahiyezere mwana wa Amisadai: chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta ukhale nsembe yaufa; chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza; ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza; tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Ahiyezere mwana wa Amisadai. Tsiku la khumi ndi limodzi kalonga wa ana a Asere, ndiye Pagiyele mwana wa Okarani; chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa; chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza; ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza; tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Pagiyele mwana wa Okarani. Tsiku lakhumi ndi chiwiri kalonga wa ana a Nafutali, ndiye Ahira mwana wa Enani: chopereka chake ndicho mbale imodzi yasiliva, kulemera kwake masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa; chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza; ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza; tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ichi ndi chopereka cha Ahira mwana wa Enani. Uku ndi kupereka chiperekere guwa la nsembe, ndi akalonga a Israele, tsiku la kudzoza kwake: mbale zasiliva khumi ndi ziwiri, mbale zowazira zasiliva khumi ndi ziwiri, zipande zagolide khumi ndi ziwiri; mbale yasiliva yonse masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, ndi mbale yowazira yonse masekeli makumi asanu ndi awiri; siliva wonse wa zotengerazo ndizo masekeli zikwi ziwiri ndi mazana anai, kuyesa sekeli wa malo opatulika. Zipande zagolide ndizo khumi ndi ziwiri, zodzala ndi chofukiza, chipande chonse masekeli khumi, kuyesa sekeli wa malo opatulika; golide wonse wa zipandezo ndiwo masekeli zana limodzi ndi makumi awiri; ng'ombe zonse za nsembe yopsereza ndizo ng'ombe khumi ndi ziwiri, nkhosa zamphongo khumi ndi ziwiri, anaankhosa a chaka chimodzi khumi ndi awiri, pamodzi ndi nsembe yao yaufa; ndi atonde a nsembe zauchimo khumi ndi awiri; ndi ng'ombe zonse za nsembe yoyamika ndizo ng'ombe makumi awiri ndi zinai, nkhosa zamphongo makumi asanu ndi limodzi, atonde makumi asanu ndi limodzi, anaankhosa a chaka chimodzi makumi asanu ndi limodzi. Uku ndi kupereka chiperekere, litadzozedwa guwa la nsembe. Ndipo polowa Mose ku chihema chokomanako, kunena ndi Iye, anamva mau akunena naye ochokera ku chotetezerapo chili pa likasa la mboni, ochokera pakati pa akerubi awiriwo; ndipo Iye ananena naye. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Nena kwa Aroni, nuti naye, Pamene uyatsa nyalizo, nyali zisanu ndi ziwirizo ziwale pandunji pake pa choikapo nyalicho. Ndipo Aroni anachita chotero; anayatsa nyalizo kuti ziwale pandunji pake pa choikapo nyali, monga Yehova adauza Mose. Ndipo mapangidwe ake a choikapo nyali ndiwo golide wosula; kuyambira tsinde lake kufikira maluwa ake anachisula; monga mwa maonekedwe ake Yehova anaonetsa Mose, momwemo anachipanga choikapo nyali. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Uwatenge Alevi pakati pa ana a Israele, nuwayeretse. Ndipo utere nao kuwayeretsa: uwawaze madzi akuchotsa zoipa, ndipo apititse lumo pa thupi lao lonse, natsuke zovala zao, nadziyeretse. Pamenepo atenge ng'ombe yamphongo ndi nsembe yake yaufa, ufa wosanganiza ndi mafuta; utengenso ng'ombe yamphongo ina ikhale nsembe yauchimo. Ndipo ubwere nao Alevi pakhomo pa chihema chokomanako; nuwasonkhanitse khamu lonse la ana a Israele; nubwere nao Alevi pamaso pa Yehova; ndi ana a Israele aike manja ao pa Alevi; ndi Aroni apereke Alevi ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova, yochokera kwa ana a Israele, kuti akhale akuchita ntchito ya Yehova, Ndipo Alevi aike manja ao pa mitu ya ng'ombezo; pamenepo ukonze imodzi ikhale nsembe yauchimo, ndi inzake, nsembe yopsereza za Yehova, kuchita chotetezera Alevi. Ndipo uimike Alevi pamaso pa Aroni, ndi pamaso pa ana ake, ndi kuwapereka ngati nsembe yoweyula kwa Yehova. Momwemo upatule Alevi mwa ana a Israele; kuti Alevi akhale anga. Ndipo atatero alowe Alevi kuchita ntchito ya chihema chokomanako; ndipo uwayeretse, ndi kuwapereka ngati nsembe yoweyula. Pakuti aperekedwa konse kwa Ine ochokera mwa ana a Israele; ndadzitengera iwo m'malo mwa onse akutsegula m'mimba, ndiwo oyamba kubadwa a ana a Israele. Pakuti oyamba kubadwa onse mwa ana a Israele ndi anga, mwa anthu ndi zoweta; tsiku lija ndinakantha oyamba kubadwa onse m'dziko la Ejipito, ndinadzipatulira iwo akhale anga. Ndipo ndatenga Alevi m'malo mwa oyamba kubadwa onse mwa ana a Israele. Ndipo ndapereka Alevi akhale mphatso ya kwa Aroni ndi ana ake amuna yochokera mwa ana a Israele, kuchita ntchito ya ana a Israele, m'chihema chokomanako ndi kuchita chotetezera ana a Israele; kuti pasakhale mliri pakati pa ana a Israele, pakuyandikiza ana a Israele ku malo opatulika. Ndipo Mose ndi Aroni ndi khamu lonse la ana a Israele anachitira Alevi monga mwa zonse Yehova adauza Mose kunena za Alevi; momwemo ana a Israele anawachitira. Ndipo Alevi anadziyeretsa, natsuka zovala zao; ndi Aroni anawapereka ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndi Aroni anawachitira chotetezera kuwayeretsa. Ndipo atatero, Alevi analowa kuchita ntchito yao m'chihema chokomanako pamaso pa Aroni, ndi pamaso pa ana ake amuna; monga Yehova anauza Mose kunena za Alevi, momwemo anawachitira. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Ichi ndi cha Alevi: kuyambira ali wa zaka makumi awiri ndi zisanu ndi mphambu azilowa kutumikira utumikiwu mu ntchito ya chihema chokomanako; ndipo kuyambira zaka makumi asanu azileka kutumikira utumikiwu, osachitanso ntchitoyi; koma atumikire pamodzi ndi abale ao m'chihema chokomanako, kusunga udikirowo, koma osagwira ntchito. Utere nao Alevi kunena za udikiro wao. Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'chipululu cha Sinai, mwezi woyamba wa chaka chachiwiri atatuluka m'dziko la Ejipito, ndi kuti, Ana a Israele achite Paska pa nyengo yoikidwa. Tsiku lakhumi ndi chinai la mweziwo, madzulo, muziuchita, pa nyengo yake yoikidwa; muuchite monga mwa malemba ake onse, ndi maweruzo ake onse. Ndipo Mose ananena ndi ana a Israele, kuti achite Paska. Ndipo anachita Paska mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chinai la mweziwo, madzulo m'chipululu cha Sinai; monga mwa zonse Yehova adauza Mose, momwemo ana a Israele anachita. Pamenepo panali amuna, anadetsedwa ndi mtembo wa munthu, ndipo sanakhoze kuchita Paska tsiku lomwelo; m'mwemo anafika pamaso pa Mose ndi pamaso pa Aroni tsiku lomwelo; nanena naye amunawa, Tadetsedwa ife ndi mtembo wa munthu; atiletseranji, kuti tisabwere nacho chopereka cha Yehova pa nyengo yake yoikidwa, pakati pa ana a Israele? Ndipo Mose ananena nao, Baimani; ndimve chouza Yehova za inu. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Nena ndi ana a Israele, ndi kuti, Angakhale munthu wa inu kapena wa mibadwo yanu, adetsedwa, chifukwa cha mtembo, kapena pokhala paulendo, koma azichitira Yehova Paska. Mwezi wachiwiri, tsiku lake lakhumi ndi chinai, madzulo, auchite; audye ndi mkate wopanda chotupitsa ndi msuzi wowawa. Asasiyeko kufikira m'mawa, kapena kuthyolapo fupa; auchite monga mwa lemba lonse la Paska. Munthu akakhala woyera, wosakhala paulendo, koma akaleka kuchita Paska, amsadze munthuyo kwa anthu a mtundu wake; popeza sanabwere nacho chopereka cha Yehova pa nyengo yake yoikidwa, munthuyu asenze kuchimwa kwake. Ndipo mlendo akakhala mwa inu, nakachitira Yehova Paska, azichita monga mwa lemba la Paska, ndi monga mwa chiweruzo chake; lemba likhale limodzi kwa inu, ndi kwa mlendo, ndi kwa wobadwa m'dziko. Ndipo tsiku loutsa Kachisi mtambo unaphimba Kachisi, ndiwo chihema chokomanako; ndicho chihema chaumboni, ndipo madzulo padaoneka pa Kachisi ngati moto, kufikira m'mawa. Kudatero kosalekeza; mtambo umachiphimba, ndi moto umaoneka usiku. Ndipo pokwera mtambo kuchokera kuchihema, utatero ana a Israele amayenda ulendo wao; ndipo pamalo pokhala mtambo, pamenepo ana a Israele amamanga mahema ao. Pakuwauza Yehova ana a Israele amayenda ulendo, powauza Yehova amamanga mahema ao; masiku onse mtambo ukakhala pamwamba pa Kachisi amakhala m'chigono. Ndipo pakukhalitsa mtambo masiku ambiri pamwamba pa Kachisi, pamenepo ana a Israele anasunga udikiro wa Yehova osayenda ulendo. Ndipo pokhala mtambo pamwamba pa Kachisi masiku pang'ono; pamenepo anakhala m'chigono monga awauza Yehova, nayendanso ulendo monga anauza Yehova. Koma mtambo ukakhala kuyambira madzulo kufikira m'mawa; pokwera mtambo m'mawa, ayenda ulendo. Ngakhale masiku awiri, kapena mwezi, kapena masiku ambiri, pokhalitsa mtambo pamwamba pa Kachisi ndi kukhalapo, ana a Israele anakhala m'chigono, osayenda ulendo; koma pakukwera uwu, anayenda ulendo. Powauza Yehova amanga mahema, powauza Yehova ayenda ulendo; anasunga udikiro wa Yehova powauza Yehova mwa dzanja la Mose. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Dzipangire malipenga awiri asiliva; uwasule mapangidwe ake; uchite nao poitana khamu, ndi poyendetsa a m'zigono. Akaliza, khamu lonse lisonkhane kuli iwe ku khomo la chihema chokomanako. Akaliza limodzi, pamenepo akalonga, akulu a zikwi a m'Israele, azisonkhana kuli iwe. Mukaliza chokweza ayende a m'zigono za kum'mawa. Mukalizanso chokweza, a m'zigono za kumwera ayende; alize chokweza pakumuka. Pomemeza msonkhano mulize, wosati chokweza ai. Ana amuna a Aroni, ansembe, ndiwo aziliza malipenga; ndipo akhale kwa inu lemba losatha ku mibadwo yanu. Ndipo pamene mupita kunkhondo m'dziko lanu kuchita nkhondo pa mdani wakusautsa inu, mulize chokweza ndi malipenga; ndipo Yehova Mulungu wanu adzakumbukira inu, nadzakupulumutsani kwa adani anu. Momwemo tsiku lakukondwera inu, ndi nyengo zoikidwa zanu, ndi poyamba miyezi yanu, muziliza malipenga pa nsembe zanu zopsereza, ndi pa nsembe zanu zoyamika; ndipo akhale kwa inu chikumbutso pamaso pa Mulungu wanu; Ine ndine Yehova Mulungu wanu. Ndipo kunachitika, chaka chachiwiri, mwezi wachiwiri, tsiku la makumi awiri la mweziwo, kuti mtambo unakwera kuchokera kwa Kachisi wa mboni. Ndipo ana a Israele anayenda monga mwa maulendo ao, kuchokera m'chipululu cha Sinai; ndi mtambo unakhala m'chipululu cha Parani. Potero anayamba ulendo wao monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose. Ndipo anayamba kuyenda ambendera ya chigono cha ana a Yuda monga mwa magulu ao; woyang'anira gulu lake ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu. Ndi pa gulu la fuko la ana a Isakara panali Netanele mwana wa Zuwara. Ndi gulu la fuko la ana a Zebuloni panali Eliyabu mwana wa Heloni. Ndipo anagwetsa Kachisi; ndi ana a Geresoni, ndi ana a Merari, akunyamula Kachisi, anamuka naye. Ndi a mbendera ya chigono cha Rubeni, anayenda monga mwa magulu ao; ndipo pa gulu lake anayang'anira Elizuri mwana wa Sedeuri. Ndi pa gulu la fuko la ana a Simeoni anayang'anira Selumiele mwana wa Zurishadai. Ndi pa gulu la fuko la ana a Gadi anayang'anira Eliyasafu mwana wa Deuwele. Pamenepo Akohati anayenda, ndi kunyamula zopatulika, ndi enawo anautsiratu Kachisi asanafike iwowa. Ndipo anayenda a mbendera ya chigono cha ana a Efuremu, monga mwa magulu ao; ndi pa gulu lake anayang'anira Elisama mwana wa Amihudi. Ndi pa gulu la fuko la ana a Manase anayang'anira Gamaliele mwana wa Pedazuri. Ndi pa gulu la fuko la ana a Benjamini anayang'anira Abidani mwana wa Gideoni. Pamenepo anayenda a mbendera ya chigono cha ana a Dani, ndiwo a m'mbuyombuyo a zigono zonse, monga mwa magulu ao; ndi pa gulu lake anayang'anira Ahiyezere mwana wa Amisadai. Ndi pa gulu la fuko la ana a Asere anayang'anira Pagiyele mwana wa Okarani. Ndi pa gulu la fuko la ana a Nafutali anayang'anira Ahira mwana wa Enani. Potero maulendo a ana a Israele anakhala monga mwa magulu ao; nayenda ulendo wao. Ndipo Mose anati kwa Hobabu mwana wa Reuwele Mmidiyani mpongozi wa Mose, Ife tili kuyenda kunka ku malo amene Yehova anati, Ndidzakupatsani awa; umuke nafe, tidzakuchitira zokoma; popeza Yehova wanenera Israele zokoma. Koma anati kwa iye, Sindidzamuka nanu; koma ndipita ku dziko langa, ndi kwa abale anga. Koma anati, Usatisiyetu; popeza udziwa poyenera kumanga ife m'chipululu, ndipo udzakhala maso athu. Ndipo kudzatero, ukamuka nafe, inde, kudzali kuti zokoma zilizonse Yehova atichitira ife, zomwezo tidzakuchitira iwe. Ndipo anayenda kuchokera kuphiri la Yehova ulendo wa masiku atatu; ndipo likasa la chipangano cha Yehova, linawatsogolera ulendo wa masiku atatu kuwafunira popumulira. Ndipo mtambo wa Yehova unali pamwamba pao msana, pakuyenda iwo kuchokera kuchigono. Ndipo kunali pakuchokera kunka nalo likasa, Mose anati, Ukani Yehova, abalalike adani anu; akuda Inu athawe pamaso panu. Ndi pakupumula ili anati, Bwerani Yehova kwa zikwizikwi za Israele. Ndipo anthu anaipa, namadandaula m'makutu a Yehova; ndipo pamene Yehova anamva anapsa mtima; ndi moto wa Yehova unayaka pakati pao, nunyeketsa ku chilekezero cha chigono. Pamenepo anthu anafuulira kwa Mose; ndi Mose anapemphera kwa Yehova, ndi motowo unazimika. Ndipo anatcha malowo dzina lake Tabera; popeza moto wa Yehova udayaka pakati pao. Ndipo anthu osokonezeka ali pakati pao anagwidwa nacho chilakolako; ndi ana a Israele omwe analiranso, nati, Adzatipatsa nyama ndani? Tikumbukira nsomba tinazidya m'Ejipito chabe, minkhaka, ndi mavwende, ndi anyezi a mitundu itatu; koma tsopano moyo wathu waphwa; tilibe kanthu pamaso pathu koma mana awa. Ndipo mana ananga zipatso zampasa, ndi maonekedwe ake ngati maonekedwe a bedola. Anthu amanka, nawaola, nawapera ndi mphero, kapena kuwasinja mumtondo, nawaphika m'mphika, nawaumba timitanda; ndi powalawa anali ngati timitanda tokazinga ndi mafuta. Ndipo pakugwa mame pachigono usiku, mana anagwapo. Ndipo Mose anamva anthu alikulira m'mabanja ao, yense pakhomo pa hema wake; ndipo Yehova anapsa mtima ndithu, ndipo kudamuipira Mose. Ndipo Mose anati kwa Yehova, Munachitiranji choipa mtumiki wanu? Ndalekeranji kupeza ufulu pamaso panu, kuti muika pa ine katundu wa anthu awa onse? Kodi ndinaima nao anthu awa onse? Kodi ndinawabala, kuti munene nane, Uwayangate ngati mlezi afukata khanda, kunka nao ku dzikolo mudalumbirira makolo ao? Ndidzaiona kuti nyama yakuwapatsa anthu awa onse? Pakuti amalirira ine, ndi kuti, Tipatseni nyama, tidye. Sinditha kuwasenza anthu awa onse ndekha, pakuti andilemera ine. Ndipo ngati mundichitira chotero, mundiphetu tsopano apa, ngati ndapeza ufulu pamaso panu, ndisayang'ane tsoka langa. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Undisonkhanitsire amuna makumi asanu ndi awiri mwa akulu a Israele, amene uwadziwa kuti ndiwo akulu a anthu, ndi akapitao ao; nubwere nao ku chihema chokomanako, kuti aimeko pamodzi ndi iwe. Pamenepo ndidzatsika ndi kulankhula nawe komweko; ndipo ndidzatengako mzimu uli pa iwe, ndi kuika pa iwowa; adzakuthandiza kusenza katundu wa anthu awa, kuti usasenze wekha. Ndipo unene ndi anthu, Mudzipatuliretu, mawa mudzadya nyama; popeza mwalira m'makutu a Yehova, ndi kuti, Adzatipatsa nyama ndani? Popeza tinakhala bwino m'Ejipito. Potero Yehova adzakupatsani nyama, ndipo mudzadya. Simudzadya tsiku limodzi, kapena masiku awiri, kapena masiku asanu, kapena masiku khumi, kapena masiku makumi awiri; koma mwezi wamphumphu, kufikira ibwera m'mphuno mwako, ndi kuti ufukidwa nayo, pakuti mwakaniza Yehova wakukhala pakati pa inu, ndi kulira pamaso pake, ndi kuti, Tinatulukiranji m'Ejipito? Ndipo Mose anati, Anthu amene ndili pakati pao, ndiwo zikwi mazana asanu ndi limodzi oyenda pansi, ndipo Inu mwanena, Ndidzawapatsa nyama, kuti adye mwezi wamphumphu. Kodi adzawaphera magulu a nkhosa ndi ng'ombe, kuwakwanira? Kapena kodi nsomba zonse za m'nyanja zidzawasonkhanira pamodzi, kuwakwanira? Ndipo Yehova anati kwa Mose, Kodi dzanja la Mulungu lafupikira? Tsopano udzapenya ngati mau anga adzakuchitikira kapena iai. Ndipo Mose anatuluka, nauza anthu mau a Yehova; nasonkhanitsa akulu a anthu makumi asanu ndi awiri, nawaimika pozungulira pa chihema. Ndipo Yehova anatsika mumtambo, nanena naye, natengako mzimu uli pa iye, nauika pa akulu makumi asanu ndi awiri; ndipo kunali kuti pokhala mzimu pa iwowa, ananenera; koma osabwerezanso. Koma amuna awiri anatsalira m'chigono, dzina la wina ndiye Elidadi, dzina la mnzake ndiye Medadi; ndipo mzimuwo unakhala pa iwo; iwo ndiwo mwa oitanidwawo, koma sanatuluke kunka kuchihema; ndipo ananenera m'chigono. Ndipo anathamanga anyamata, nauza Mose, nati, Elidadi ndi Medadi alikunenera m'chigono. Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Mose kuyambira ubwana wake, anayankha nati, Mose, mfumu yanga, aletseni. Koma Mose anati kwa iye, Kodi uchita nsanje nao chifukwa cha ine? Mwenzi anthu onse a Yehova atakhala aneneri? Mwenzi Yehova atawaikira mzimu wake! Ndipo Mose ndi akulu onse a Israele anasonkhana kuchigono. Ndipo kudachokera mphepo kwa Yehova, nidza nazo zinziri zochokera kunyanja, nizitula kuchigono, ulendo wa tsiku limodzi dera lino, ndi ulendo wa tsiku limodzi dera lina, pozungulira pa chigono, ndipo zinabisa nthaka ngati muyeso wa mikono iwiri. Ndipo anthu anauka tsiku lonselo, ndi usiku wake wonse, ndi mawa lake lonse, nakusa zinzirizo; wokusa pang'ono anakusa zodzaza mahomeri khumi; ndipo anadziyanikira izi pozungulira pa chigono. Nyamayi ikali pakati pa mano, asanaitafune, Mulungu anapsa mtima pa anthuwa, ndipo Yehova anawakantha anthu ndi kukantha kwakukulu ndithu. Ndipo anatcha malowo dzina lake Kibroti-Hatava; popeza pamenepo anaika anthu osusuka. Kuchokera ku Kibroti-Hatava anthuwo anayenda kunka ku Hazeroti; nakhala ku Hazeroti. Ndipo Miriyamu ndi Aroni anatsutsana naye Mose chifukwa cha mkazi mtundu wake Mkusi amene adamtenga; popeza adatenga mkazi Mkusi. Ndipo anati, Kodi Yehova wanena ndi Mose yekha? Sananenanso ndi ife nanga? Ndipo Yehova anamva. Koma munthuyu Mose ndiye wofatsa woposa anthu onse a pa dziko lapansi. Ndipo Yehova anati kwa Mose, ndi Aroni, ndi Miriyamu modzidzimutsa, Tulukani inu atatu kudza ku chihema chokomanako. Pamenepo anatuluka atatuwo. Ndipo Yehova anatsika mumtambo njo, naima pa khomo la chihema, naitana Aroni ndi Miriyamu; natuluka onse awiri. Ndipo anati, Tamvani, tsono mau anga; pakakhala mneneri pakati pa inu, Ine Yehova ndidzizindikiritsa kwa iye m'masomphenya, ndinena naye m'kulota. Satero mtumiki wanga Mose; ndiye wokhulupirika m'nyumba mwanga monse. Ndimanena naye pakamwa ndi pakamwa, moonekera, osati mophiphiritsa; ndipo amapenyerera maonekedwe a Yehova; potero munalekeranji kuopa kutsutsana naye mtumiki wanga, Mose. Pamenepo Yehova anawapsera mtima iwo; nawachokera Iye. Ndipo mtambo unachoka pachihema; ndipo taonani, Miriyamu anali wakhate, wa mbu ngati chipale chofewa; ndipo Aroni anapenya Miriyamu, taonani, anali wakhate. Ndipo Aroni anati kwa Mose, Mfumu yanga, musatiikiretu kuchimwa kumene tapusa nako, ndi kuchimwa nako. Asakhaletu iye ngati wakufa, amene dera lina la mnofu wake watha potuluka iye m'mimba mwa make. Ndipo Mose anafuulira kwa Yehova, ndi kuti, Mchiritsenitu, Mulungu. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Atate wake akadamlavulira malovu pankhope pake sakadachita manyazi masiku asanu ndi awiri? Ambindikiritse kunja kwa chigono masiku asanu ndi awiri; ndipo atatero amlandirenso. Pamenepo anambindikiritsa Miriyamu kunja kwa chigono masiku asanu ndi awiri; ndipo anthu sanayende ulendo kufikira atamlandiranso Miriyamu. Ndipo atatero anthuwo ananka ulendo wao kuchokera ku Hazeroti, namanga mahema ao m'chipululu cha Parani. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Udzitumire amuna, kuti azonde dziko la Kanani, limene ndilikupatsa ana a Israele; utumize munthu mmodzi wa fuko lililonse la makolo ao, yense kalonga pakati pa anzake. Ndipo Mose anawatumiza kuchokera ku chipululu cha Parani monga mwa mau a Yehova; amuna onsewa ndiwo akulu a ana a Israele. Maina ao ndi awa: wa fuko la Rubeni, Samuwa mwana wa Zakuri. Wa fuko la Simeoni, Safati mwana wa Hori. Wa fuko la Yuda, Kalebe mwana wa Yefune. Wa fuko la Isakara, Igala mwana wa Yosefe. Wa fuko la Efuremu, Hoseya mwana wa Nuni. Wa fuko la Benjamini, Paliti mwana wa Rafu. Wa fuko la Zebuloni, Gadiele mwana wa Sodi. Wa fuko la Yosefe, wa fuko la Manase, Gadi mwana wa Susi. Wa fuko la Dani, Amiyele mwana wa Gemali. Wa fuko la Asere, Seturi mwana wa Mikaele. Wa fuko la Nafutali, Nabi mwana wa Vofusi. Wa fuko la Gadi, Geuwele mwana wa Maki. Awa ndi maina a amunawo Mose anawatumira azonde dziko. Ndipo Mose anamutcha Hoseya mwana wa Nuni Yoswa. Potero Mose anawatuma azonde dziko la Kanani, nanena nao, Kwerani uko kumwera, nimukwere kumapiri; mukaone dziko umo liliri; ndi anthu akukhala m'mwemo, ngati ali amphamvu kapena ofooka, ngati achepa kapena achuluka; ndi umo liliri dzikoli lokhalamo iwo, ngati lokoma, kapena loipa; ndi umo iliri midziyo akhalamo iwo, ngati akhala poyera kapena m'malinga; ndi umo iliri nthaka, ngati yopatsa, kapena yosuka, ngati pali mitengo, kapena palibe. Ndipo limbikani mtima, nimubwere nazo zipatso za m'dzikomo. Koma nyengoyi ndiyo nyengo yoyamba kupsa mphesa. Pamenepo anakwerako, nazonda dziko kuyambira chipululu za Zini kufikira Rehobu, polowa ku Hamati. Ndipo anakwera njira ya kumwera nafika ku Hebroni; ndi apa panali Ahimani, Sesai, ndi Talimai, ana a Anaki. (Koma atamanga Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri ndipo anamanga Zowani m'Ejipito.) Ndipo anadza ku chigwa cha Esikolo, nachekako tsango limodzi la mphesa, nalisenza awiri mopika; anabwera nazonso makangaza ndi nkhuyu. Malowa anawatcha chigwa cha Esikolo, chifukwa cha tsangolo ana a Israele analichekako. Pamenepo anabwerera atazonda dziko, atatha masiku makumi anai. Ndipo anamuka, nadza kwa Mose, ndi Aroni, ndi khamu lonse la ana a Israele, ku chipululu cha Parani ku Kadesi; ndipo anabwezera mau iwowa, ndi khamu lonse, nawaonetsa zipatso za dzikoli. Ndipo anafotokozera, nati Tinakafika ku dziko limene munatitumirako, ndilo ndithu moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ndi zipatso zake siizi. Komatu anthu okhala m'dzikomo ngamphamvu; ndi midziyo nja malinga, yaikulu ndithu; ndipo tinaonakonso ana a Anaki. Aamaleke akhala m'dziko la kumwera; ndi Ahiti, ndi Ayebusi, ndi Aamori, akhala ku mapiri, ndi Akanani akhala kunyanja, ndi m'mphepete mwa Yordani. Koma Kalebe anatontholetsa anthu pamaso pa Mose, nati, Tikwere ndithu ndi kulilandira lathulathu; popeza tikhozadi kuchita kumene. Koma anthu adakwera nayewo anati, Sitikhoza kuwakwerera anthuwo; popeza atiposa mphamvu. Ndipo anaipsira ana a Israele mbiri ya dziko adalizonda, ndilo dziko lakutheramo anthu okhalamo; ndi anthu onse tidaona pakati pake ndiwo anthu aatali misinkhu. Tinaonakonso Anefili, ana a Anaki, obadwa ndi Anefili; ndipo tinaoneka m'maso mwathu ngati ziwala; momwemonso tinaoneka m'maso mwao. Pamenepo khamu lonse linakweza mau ao, nafuula; ndipo anthuwo analira usikuwo. Ndipo ana onse a Israele anadandaulira Mose ndi Aroni; ndi khamu lonse linanena nao, Mwenzi tikadafa m'dziko la Ejipito; kapena mwenzi tikadafa m'chipululu muno! Ndipo Yehova atitengeranji kudza nafe kudziko kuno, kuti tigwe nalo lupanga? Akazi athu ndi makanda athu adzakhala chakudya chao; kodi sikuli bwino tibwerere ku Ejipito? Ndipo anati wina ndi mnzake, Tiike mtsogoleri, tibwerere ku Ejipito. Pamenepo Mose ndi Aroni anagwa nkhope pansi pamaso pa msonkhano wonse wa khamu la ana a Israele. Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, ndi Kalebe mwana wa Yefune, ndiwo a iwo aja adazonda dzikolo, anang'amba zovala zao; nanena ndi khamu lonse la ana a Israele, nati, Dziko tapitamo kulizonda, ndilo dziko lokometsetsa ndithu. Yehova akakondwera nafe, adzatilowetsa m'dzikomo, ndi kutipatsa ilo; ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi. Chokhachi musamapikisana naye Yehova, musamaopa anthu a m'dzikomo; pakuti ndiwo mkate wathu; mthunzi wao wawachokera, ndipo Yehova ali nafe; musamawaopa. Koma khamu lonse lidati liwaponye miyala. Ndipo ulemerero wa Yehova unaoneka m'chihema chokomanako kwa ana onse a Israele. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Anthu awa adzaleka liti kundinyoza? Ndipo adzayamba liti kundikhulupirira, chinkana zizindikiro zonse ndinazichita pakati pao? Ndidzawakantha ndi mliri, ndi kuwachotsera cholowa chao, ndipo ndidzakusandutsa iwe mtundu wa anthu waukulu ndi wamphamvu koposa iwowa. Ndipo Mose anati kwa Yehova, Pamenepo Aejipito adzamva; popeza munakweza anthu awa ndi mphamvu yanu kuwachotsa pakati pao; ndipo adzawauza okhala m'dziko muno; adamva kuti inu Yehova muli pakati pa anthu awa; pakuti muoneka mopenyana, Yehova ndi mtambo wanu umaima pamwamba pao, ndipo muwatsogolera, ndi mtambo njo msana, ndi moto njo usiku. Ndipo mukapha anthu awa ngati munthu mmodzi, pamenepo amitundu amene adamva mbiri yanu adzanena, ndi kuti, Popeza Yehova sanakhoze kuwalowetsa anthu awa m'dziko limene anawalumbirira, chifukwa chake anawapha m'chipululu. Ndipo tsopano, ikuletu mphamvu ya Mbuye wanga, monga mudanena, ndi kuti, Yehova ndiye wolekereza, ndi wa chifundo chochuluka, wokhululukira mphulupulu ndi kulakwa, koma wosamasula wopalamula; wakuwalanga ana chifukwa cha mphulupulu ya atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai. Khululukiranitu mphulupulu ya anthu awa, monga mwa chifundo chanu chachikulu, ndi monga mudalekerera anthu awa, kuyambira Ejipito kufikira tsopano. Ndipo Yehova anati, Ndakhululukira monga mwa mau ako: koma ndithu, pali Ine, dziko lonse lapansi lidzadzazidwa ndi ulemerero wa Yehova; popeza anthu onse awa amene adaona ulemerero wanga, ndi zizindikiro zanga, ndidazichita m'Ejipito ndi m'chipululu, koma anandiyesa Ine kakhumi aka, osamvera mau anga; sadzaona dzikoli ndidalumbirira makolo ao, ngakhale mmodzi wa iwo akundinyoza Ine, sadzaliona; koma mtumiki wanga Kalebe, popeza anali nao mzimu wina, nanditsata monsemo, ndidzamlowetsa iyeyu m'dziko muja analowamo; ndi mbeu zake zidzakhala nalo. Koma Aamaleke ndi Akanani akhala m'chigwamo; tembenukani mawa, nimumke ulendo wanu kuchipululu, njira ya ku Nyanja Yofiira. Ndipo Yehova ananena kwa Mose ndi Aroni, nati, Ndileke khamu loipa ili lakudandaula pa Ine kufikira liti? Ndidamva madandaulo a ana a Israele, amene amandidandaulira. Nunene nao, Pali Ine ati Yehova, ndidzachitira inu ndithu monga mwanena m'makutu mwanga; mitembo yanu idzagwa m'chipululu muno; ndi owerengedwa anu onse, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, akudandaula pa Ine; simudzalowa inu m'dzikolo, ndinakwezapo dzanja langa kukukhalitsani m'mwemo, koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni ndiwo. Koma makanda anu, amene munanena za iwowa kuti adzakhala chakudya, amenewo ndidzawalowetsa, ndipo adzadziwa dzikolo mudalikana. Koma inu, mitembo yanu idzagwa m'chipululu muno. Ndipo ana anu adzakhala oyendayenda m'chipululu zaka makumi anai, nadzasenza kupulukira kwanu, kufikira mitembo yanu yatha m'chipululu. Monga mwa kuwerenga kwa masiku amene munazonda dziko, masiku makumi anai, tsiku limodzi kuwerenga chaka chimodzi, mudzasenza mphulupulu zanu, zaka makumi anai, ndipo mudzadziwa kuti ndaleka lonjezano langa. Ine Yehova ndanena, ndidzachitira ndithu ichi khamu ili lonse loipa lakusonkhana kutsutsana nane; adzatha m'chipululu muno, nadzafamo. Ndipo amunawo, amene Mose anawatumiza kukazonda dziko, amene anabwera nadandaulitsa khamu lonse pa iye, poipsa mbiri ya dziko, amuna amene anaipsa mbiri ya dziko, anafa ndi mliri pamaso pa Yehova. Koma Yoswa mwana wa Nuni, ndi Kalebe mwana wa Yefune, anakhala ndi moyo mwa amuna aja adamukawo kukazonda dziko. Ndipo Mose anauza ana a Israele mau onse awa; ndipo anthu anamva chisoni chambiri. Ndipo anauka mamawa, nakwera pamwamba pa phiri, nati, Tili pano, tidzakwera kunka ku malo amene Yehova ananena; popeza tachimwa. Ndipo Mose anati, Mutero chifukwa ninji kulakwira mau a Yehova, popeza simudzapindula nako? Musakwereko, pakuti Yehova sali pakati pa inu; kuti angakukantheni adani anu. Pakuti Aamaleke ndi Akanani ali komweko patsogolo panu, ndipo mudzagwa ndi lupanga; popeza mwabwerera m'mbuyo osatsata Yehova, chifukwa chake Yehova sadzakhala nanu. Koma anakwera pamwamba pa phiri modzikuza; koma likasa la chipangano la Yehova, ndi Mose, sanachoke kuchigono. Pamenepo anatsika Aamaleke, ndi Akanani, akukhala m'phirimo nawakantha, nawapha kufikira ku Horoma. Ndipo Yehova ananena ndi Mose nati, Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mukakalowa m'dziko lokakhalamo inu, limene ndilikupatsa inu, ndipo mukakonzera Yehova nsembe yamoto, nsembe yopsereza, kapena yophera, pochita chowinda cha padera, kapena nsembe yaufulu, kapena nsembe ya pa nyengo zanu zoikika, kumchitira Yehova fungo lokoma, la ng'ombe kapena nkhosa; pamenepo iye wobwera nacho chopereka chake kwa Yehova, azibwera nayo nsembe yaufa, limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wosalala, wosanganiza ndi limodzi la magawo anai la hini la mafuta; ndipo uzikonzera nsembe yopsereza kapena yophera, vinyo wa nsembe yothira, limodzi la magawo anai la hini, ukhale wa mwanawankhosa mmodzi. Kapena ukonzere nkhosa yamphongo nsembe yaufa, awiri mwa magawo khumi a efa wa ufa wosalala, wosanganiza ndi mafuta, limodzi la magawo atatu la hini. Ndipo ubwere naye vinyo wa nsembe yothira, limodzi la magawo atatu la hini, achitire Yehova fungo lokoma. Ndipo pamene mukonza ng'ombe ikhale nsembe yopsereza, kapena yophera, kuchita chowinda cha padera, kapena ikhale nsembe yoyamika ya Yehova; abwere nayo, pamodzi ndi ng'ombeyo, nsembe ya efa wa ufa wosalala, atatu mwa magawo khumi wosanganiza ndi mafuta, limodzi la magawo awiri la hini. Ndipo ubwere naye vinyo wa nsembe yothira limodzi la magawo awiri la hini, ndiye nsembe yamoto ya fungo lokoma, ya Yehova. Kudzatero ndi ng'ombe iliyonse, kapena nkhosa yamphongo iliyonse, kapena mwanawankhosa aliyense, kapena mwanawambuzi aliyense. Monga mwa kuwerenga kwake kwa izi muzikonza, muzitero ndi yonse monga mwa kuwerenga kwake. Onse akubadwa m'dzikomo achite izi momwemo, pobwera nayo kwa Yehova nsembe yamoto ya fungo lokoma. Ndipo akakhala nanu mlendo, kapena aliyense wakukhala pakati pa inu mwa mibadwo yanu, nakachitira Yehova nsembe yamoto ya fungo lokoma; monga muchita inu, momwemo iyenso, Kunena za khamu, pakhale lemba limodzi kwa inu, ndi kwa mlendo wakukhala kwanu, ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu; monga mukhala inu, momwemo mlendo pamaso pa Yehova. Pakhale chilamulo chimodzi ndi chiweruzo chimodzi kwa inu ndi kwa mlendo wakukhala kwanu. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Pamene mulowa m'dziko limene ndilikukulowetsani, kudzali, pakudya inu mkate wa m'dzikolo, muzikwezera Yehova nsembe yokweza. Pa mtanda wanu woyamba muperekeko kamtanda, kakhale nsembe yokweza; monga mumachitira nsembe yokweza ya popuntha tirigu, momwemo muzikakweza, Muzipatsa Yehova nsembe yokweza yoitenga ku mtanda wanu woyamba, mwa mibadwo yanu. Ndipo pamene mulakwa, osachita mau awa onse amene Yehova ananena ndi Mose; ndizo zonse Yehova anakuuzani ndi dzanja la Mose, kuyambira tsikulo Yehova anauza, ndi kunkabe m'mibadwo yanu; pamenepo kudzali, ngati anachichita osati dala, osachidziwa khamulo, khamu lonse lipereke ng'ombe yamphongo ikhale nsembe yopsereza, ya fungo lokoma ya Yehova, pamodzi ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira, monga mwa chiweruzo chake; ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo. Ndipo wansembe azichita chotetezera khamu lonse la ana a Israele, ndipo adzakhululukidwa; popeza sanachite dala, ndipo anadza nacho chopereka chao, nsembe yamoto kwa Yehova, ndi nsembe yao yauchimo pamaso pa Yehova, chifukwa cha kulakwa osati dala. Ndipo khamu lonse la ana a Israele, adzakhululukidwa, ndi mlendo yemwe wakukhala pakati pao; popeza khamu lonse linachichita osati dala. Ndipo akachimwa munthu mmodzi osati dala, abwere nayo mbuzi yamsoti ya chaka chimodzi, ikhale nsembe yauchimo. Ndipo wansembe achite chomtetezera munthu wakulakwa, osalakwa dala pamaso pa Yehova, kumchita chomtetezera; ndipo adzakhululukidwa. Kunena za wobadwa m'dziko mwa ana a Israele, ndi mlendo wakukhala pakati pao, mukhale nacho chilamulo chimodzi kwa iye wakuchita kanthu kosati dala. Koma munthu wakuchita kanthu dala, ngakhale wobadwa m'dziko kapena mlendo, yemweyo achitira Yehova mwano; ndipo munthuyo amsadze pakati pa anthu a mtundu wake. Popeza ananyoza mau a Yehova, nathyola lamulo lake; munthuyu amsadze konse; mphulupulu yake ikhale pa iye. Ndipo pokhala ana a Israele m'chipululu, anapeza munthu wakufuna nkhuni tsiku la Sabata. Ndipo amene adampezawo alinkufuna nkhuni anabwera naye kwa Mose ndi Aroni, ndi kwa khamu lonse. Ndipo anathanga wamsunga, popeza sichinanenedwa choyenera kumchitira iye. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Amuphe munthuyu ndithu; khamu lonse limponye miyala kunja kwa chigono. Pamenepo khamu lonse linamtulutsa kunja kwa chigono, ndi kumponya miyala, ndipo anafa; monga Yehova adauza Mose. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Nena ndi ana a Israele, nuwauze kuti adziombere mphonje m'mphepete mwa zovala zao, mwa mibadwo yao, naike pamphonje m'mphepetemo thonje lamadzi. Ndipo chikhale kwa inu mphonje, yakuti muziyang'anirako, ndi kukumbukira malamulo onse a Yehova, ndi kuwachita, ndi kuti musamazondazonda kutsata za m'mtima mwanu, ndi za m'maso mwanu zimene mumatsata ndi chigololo; kuti mukumbukire ndi kuchita malamulo anga onse, ndi kukhala wopatulikira Mulungu wanu. Ine ndine Yehova Mulungu wanu, wakukutulutsani m'dziko la Ejipito, kuti ndikhale Mulungu wanu; Ine ndine Yehova Mulungu wanu. Koma Kora, mwana wa Izihara, mwana wa Kohati, mwana wa Levi, anatenga Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu, ndi Oni mwana wa Peleti, ana a Rubeni; ndipo anauka pamaso pa Mose, pamodzi ndi amuna mazana awiri mphambu makumi asanu a ana a Israele, ndiwo akalonga a khamulo, oitanidwa a msonkhano, amuna omveka. Ndipo anasonkhana motsutsana pa Mose ndi Aroni, nanena nao, Mukula mphamvu inu, pakuti khamu lonse nlopatulika, onsewa, ndipo Yehova ali pakati pao; mudzikuza bwanji pa msonkhano wa Yehova? Pamene Mose anamva ichi anagwa nkhope yake pansi; nanena ndi Kora ndi khamu lake lonse, ndi kuti, M'mawa Yehova adzatizindikiritsa anthu ake ndi ayani, wopatulika ndani, amene adzamsendeza pafupi pa Iye; ndi iye amene anamsankha adzamsendeza pafupi pa Iye. Chitani ichi; dzitengereni mbale za zofukiza, Kora, ndi khamu lake lonse; nimuikemo moto, muikenso chofukiza pamenepo, pamaso pa Yehova, mawa; ndipo kudzali kuti amene Yehova amsankha, wopatulika ndiye; mwakula mphamvu, inu ana a Levi. Ndipo Mose ananena ndi Kora, Tamvani tsono, inu ana a Levi; kodi muchiyesa chinthu chaching'ono, kuti Mulungu wa Israele anakusiyanitsani ku khamu la Israele, kukusendezani pafupi pa Iye, kuchita ntchito ya Kachisi wa Yehova, ndi kuima pamaso pa khamu kuwatumikira; ndi kuti anakusendeza iwe, ndi abale ako onse, ana a Levi, pamodzi ndi iwe? Ndipo kodi mufunanso ntchito ya nsembe? Chifukwa chake, iwe ndi khamu lonse mwasonkhana kutsutsana ndi Yehova; ndipo Aroniyo ndani, kuti mudandaule pa iye? Ndipo Mose anatuma kukaitaniza Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu; koma anati, Sitifikako: kodi ndi chinthu chaching'ono kuti watikweza kutichotsa m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, kutipha m'chipululu; koma udziyesanso ndithu kalonga wa ife? Ndiponso sunatilowetsa m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, kapena kutipatsa cholowa cha minda, ndi minda yamphesa; kodi udzakolowola amuna awa maso ao: Sitifikako. Pamenepo Mose adapsa mtima, ndipo anati kwa Yehova, Musasamalira chopereka chao; sindinalanda bulu wao mmodzi, kapena kuchitira choipa mmodzi wa iwowa. Ndipo Mose anati kwa Kora, Iwe ndi khamu lako lonse mukhale pamaso pa Yehova mawa, iwe ndi iwowa, ndi Aroni; nimutenge munthu yense mbale yake yofukizamo, nimuike chofukiza m'mwemo, nimubwere nazo, yense mbale yake yofukizamo pamaso pa Yehova, mbale zofukizamo mazana awiri ndi makumi asanu; ndi iwe, ndi Aroni, yense mbale yake yofukizamo. Potero munthu yense anatenga mbale yake yofukizamo, naikamo moto, naikapo chofukiza, naima pa khomo la chihema chokomanako pamodzi ndi Mose ndi Aroni. Ndipo Kora anasonkhanitsa khamu lonse mopikisana nao ku khomo la chihema chokomanako; ndipo ulemerero wa Yehova unaoneka kwa khamu lonse. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati, Dzipatuleni pakati pa khamu lino, kuti ndiwathe m'kamphindi. Ndipo anagwa nkhope zao pansi, nati, Mulungu, ndinu Mulungu wa mizimu ya anthu onse, walakwa munthu mmodzi, ndipo kodi mukwiya nalo khamu lonse? Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Nena ndi khamulo, ndi kuti, Kwerani kuchoka pozungulira mahema a Kora, Datani, ndi Abiramu. Ndipo Mose anauka namuka kwa Datani ndi Abiramu; ndi akulu a Israele anamtsata. Ndipo ananena ndi khamulo, nati, Chokanitu ku mahema a anthu awa oipa, musamakhudza kanthu kao kalikonse, mungaonongeke m'zochimwa zao zonse. Potero anakwera kuchokera pozungulira mahema a Kora, Datani, ndi Abiramu, ndipo Datani ndi Abiramu anatuluka, naima pakhomo pa mahema ao, ndi akazi ao, ndi ana ao amuna, ndi makanda ao. Ndipo Mose anati, Ndi ichi mudzadziwa kuti Yehova wanditumiza ine kuchita ntchito izi zonse, ndi kuti sizifuma m'mtima mwangamwanga. Akafa anthu awa monga amafa anthu onse, kapena akasungika monga amasungika anthu onse, Yehova sananditumize ine. Koma Yehova akalenga chinthu chatsopano, ndi nthaka ikayasama pakamwa pake, nikawameza ndi zonse ali nazo, nakatsikira iwo kumanda ali ndi moyo; pamenepo mudzadziwa kuti anthu awa anyoza Mulungu. Ndipo kunali, pakutha iye kunena mau awa onse, nthaka inang'ambika pansi pao; ndi dziko linayasama pakamwa pake ndi kuwameza, iwo ndi mabanja ao, ndi amuna ao onse akutsata Kora, ndi akatundu ao onse. Chomwecho iwowa, ndi onse anali nao, anatsikira kumanda ali ndi moyo, ndi dziko linasunama pa iwo, ndipo anaonongeka pakati pa msonkhano. Ndipo Aisraele onse akukhala pozinga pao anathawa pakumva kufuula kwao; pakuti anati, Lingatimeze dziko ifenso. Ndipo moto unatuluka kwa Yehova, ndi kunyeketsa amuna mazana awiri ndi makumi asanu aja akubwera nacho chofukiza. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Nena ndi Eleazara mwana wa Aroni wansembe, kuti aphule mbale zofukiza pakati pa moto, nutaye makalawo uko kutali: pakuti zili zopatulika; mbale zofukizazo za iwo amene adachimwira moyo waowao, ndipo azisule zaphanthiphanthi, zikhale chivundikiro cha guwa la nsembe; popeza anabwera nazo pamaso pa Yehova, chifukwa chake zikhala zopatulika; ndipo zidzakhala chizindikiro kwa ana a Israele. Ndipo Eleazara wansembe anatenga mbale zofukiza zamkuwa, zimene anthu opsererawo adabwera nazo; ndipo anazisula zaphanthiphanthi zikhale chivundikiro cha guwa la nsembe; chikhale chikumbutso kwa ana a Israele, kuti mlendo, wosati wa mbeu ya Aroni, asasendere kuchita chofukiza pamaso pa Yehova; angakhale monga Kora ndi khamu lake; monga Yehova adanena naye ndi dzanja la Mose. Koma m'mawa mwake khamu lonse la ana a Israele anadandaula pa Mose ndi Aroni, nati, Mwapha anthu a Yehova, inu. Ndipo kunali, posonkhanidwa khamulo kutsutsana nao Mose ndi Aroni, kuti anacheukira chihema chokomanako; taonani, mtambo unachiphimba, ndi ulemerero wa Yehova unaoneka. Ndipo Mose ndi Aroni anadza kukhomo kwa chihema chokomanako. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Kwerani kuchoka pakati pa khamu lino, kuti ndiwathe m'kamphindi. Pamenepo adagwa nkhope zao pansi. Ndipo Mose anati kwa Aroni, Tenga mbale yako yofukiza, nuikemo moto wa ku guwa la nsembe, nuikepo chofukiza, nufulumire kumuka ku khamulo, nuwachitire chowatetezera; pakuti watuluka mkwiyo pamaso pa Yehova; wayamba mliri. Ndipo Aroni anatenga monga Mose adanena, nathamanga kulowa pakati pa msonkhano; ndipo taonani, udayamba mliri pakati pa anthu; ndipo anaikapo chofukiza nawachitira anthu chowatetezera. Ndipo anaima pakati pa akufa ndi amoyo; ndi mliri unaleka. Koma akufa nao mliri ndiwo zikwi khumi ndi zinai mphambu mazana asanu ndi awiri, osawerenga aja adafera chija cha Kora. Ndipo Aroni anabwera kwa Mose ku khomo la chihema chokomanako; ndi mliri unaleka. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Nena ndi ana a Israele, nulandire kwa yense ndodo, banja lililonse la makolo ndodo imodzi, mtsogoleri wa mafuko ao onse monga mwa mabanja a makolo ao azipereka ndodo, zikhale khumi ndi ziwiri; nulembe dzina la yense pa ndodo yake. Ndipo ulembe dzina la Aroni pa ndodo ya Levi; pakuti pakhale ndodo imodzi pa mkulu yense wa nyumba za makolo ao. Ndipo uziike m'chihema chokomanako, chakuno cha mboni, kumene ndikomana ndi inu. Ndipo kudzali, kuti ndodo ya munthu ndimsankheyo, idzaphuka; ndipo ndidzadziletsera madandaulo a ana a Israele amene adandaula nao pa inu. Ndipo Mose ananena ndi ana a Israele, ndipo akalonga ao onse anapereka, yense ndodo imodzi, monga mwa mabanja a makolo ao, ndodo khumi ndi ziwiri; ndi ndodo ya Aroni inakhala pakati pa ndodo zao. Ndipo Mose anaika ndodozo pamaso pa Yehova m'chihema cha mboni. Ndipo kunali m'mawa mwake, kuti Mose analowa m'chihema cha mboni; ndipo taonani, ndodo ya Aroni, ya pa banja la Levi, inaphuka, nionetsa timaani, nichita maluwa, nipatsa akatungurume. Ndipo Mose anatulutsa ndodo zonse kuzichotsa pamaso pa Yehova, azione ana onse a Israele; ndipo anapenya, natenga yense ndodo yake. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Bweza ndodo ya Aroni kuiika chakuno cha mboni, isungike ikhale chizindikiro cha pa ana opikisana; kuti unditsirizire madandaulo ao, kuti ungafe. Ndipo Mose anachita monga Yehova adamuuza, momwemo anachita. Pamenepo ana a Israele ananena ndi Mose, nati, Taonani, tikufa, tionongeka, tionongeka tonse. Yense wakuyandikiza Kachisi wa Yehova amwalira; kodi tidzatha nkufa? Ndipo Yehova anati kwa Aroni, Iwe ndi ana ako amuna ndi banja la kholo lako pamodzi ndi iwe muzisenza mphulupulu ya malo opatulika; ndipo iwe ndi ana ako amuna pamodzi ndi iwe musenze mphulupulu ya ntchito yanu ya nsembe. Ndiponso abale ako, fuko la Alevi, fuko la kholo lako, uwayandikizitse pamodzi ndi iwe, kuti aphatikane ndi iwe, ndi kukutumikira; koma iwe ndi ana ako pamodzi ndi iwe mukhale ku khomo la chihema cha mboni. Ndipo asunge udikiro wako, ndi udikiro wa chihema chonse; koma asayandikize zipangizo za malo opatulika, ndi guwa la nsembe, kuti mungafe, iwo ndi inu. Koma aziphatikana nawe, nazisunga udikiro wa chihema chokomanako, kuchita ntchito yonse ya chihema; koma mlendo asayandikize inu. Ndipo musunge udikiro wa malo opatulika, ndi udikiro wa guwa la nsembe; kuti pasakhalenso mkwiyo pa ana a Israele. Ndipo Ine, taonani, ndinatenga abale anu Alevi kuwachotsa pakati pa ana a Israele; ndiwo mphatso yanu, yopatsidwa kwa Yehova, kuchita ntchito ya chihema chokomanako. Ndipo iwe ndi ana ako amuna pamodzi ndi iwe muchite ntchito yanu ya nsembe, pa zonse za ku guwa la nsembe, ndi za m'kati mwa nsalu yotchinga; ndipo mutumikire; ndikupatsani ntchito yanu ya nsembe, utumiki wopatsika kwaulere; koma mlendo wakuyandikiza amuphe. Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Ndipo taona, Ine ndakupatsa udikiro wa nsembe zanga zokweza, ndizo zopatulika zonse za ana a Israele; chifukwa cha kudzozedwaku ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako amuna, likhale lemba losatha. Izi ndi zako pa zinthu zopatulika kwambiri, zosafika kumoto; zopereka zao zonse, ndi nsembe zao zonse zaufa, ndi nsembe zao zonse zauchimo, ndi nsembe zao zonse zopalamula, zimene andibwezera Ine, zikhale zopatulika kwambiri za iwe ndi za ana ako amuna. Muzizidya izi monga zopatulika kwambiri; mwamuna yense adyeko; uziyese zopatulika. Zako ndi izinso: nsembe yokweza ya mphatso yao, ndi nsembe zoweyula zonse za ana a Israele; ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako amuna ndi kwa ana ako akazi pamodzi ndi iwe, likhale lemba losatha; oyera onse a m'banja lako adyeko. Mafuta onse okometsetsa, ndi vinyo watsopano, ndi tirigu yense wokometsetsa. Zipatso zao zoyamba zimene aziperekako kwa Yehova, ndazipereka kwa iwe. Zipatso zoyamba zonse zili m'dziko mwao, zimene amadza nazo kwa Yehova, zikhale zako; oyera onse a m'banja lako adyeko. Zilizonse zoperekedwa chiperekere m'Israele ndi zako. Zilizonse zoyambira kubadwa mwa zamoyo zonse zimene abwera nazo kwa Yehova, mwa anthu ndi mwa nyama, ndi zako; koma munthu woyamba kubadwa uzimuombola ndithu; ndi nyama yodetsa yoyamba kubadwa uziiombola. Ndipo zimene ziti zidzaomboledwa uziombole kuyambira za mwezi umodzi, monga mwa kuyesa kwako, pa ndalama za masekeli asanu, kuyesa sekeli wa malo opatulika, ndiwo magera makumi awiri. Koma ng'ombe yoyamba kubadwa, kapena nkhosa yoyamba kubadwa, kapena mbuzi yoyamba kubadwa, usaziombola; ndizo zopatulika; uwaze mwazi wake pa guwa la nsembe, ndi kufukiza mafuta ao, nsembe yamoto ya fungo lokoma kwa Yehova. Ndipo nyama yake ndi yako, ndiyo nganga ya nsembe yoweyula ndi mwendo wathako wa kulamanja, ndizo zako. Nsembe zokweza zonse za zinthu zopatulika, zimene ana a Israele azikweza kwa Yehova, ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako amuna ndi kwa ana ako akazi pamodzi ndi iwe, likhale lemba losatha; ndilo pangano lamchere losatha, pamaso pa Yehova, kwa iwe ndi mbeu zako pamodzi ndi iwe. Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Ulibe cholowa m'dziko lao, ulibe gawo pakati pao; Ine ndine gawo lako ndi cholowa chako pakati pa ana a Israele. Ndipo taonani, ndawaninkha ana a Levi limodzi la magawo khumi mwa zonse m'Israele, likhale cholowa chao, mphotho ya pa ntchito yao alikuichita, ntchito ya chihema chokomanako. Ndipo kuyambira tsopano ana a Israele asayandikize chihema chokomanako, angamasenze uchimo kuti angafe. Koma Alevi azichita ntchito ya chihema chokomanako, iwo ndiwo azisenza mphulupulu yao; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu; ndipo asakhale nacho cholowa pakati pa ana a Israele. Popeza ndapatsa Alevi limodzi la magawo khumi, la ana a Israele, limene apereka nsembe yokweza kwa Yehova, likhale cholowa chao; chifukwa chake ndanena nao, Asadzakhale nacho cholowa mwa ana a Israele. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Unenenso ndi Alevi, nuti nao, Pamene mulandira kwa ana a Israele, limodzi la magawo khumi limene ndakupatsani likhale cholowa chanu chochokera kwao, muziperekako nsembe yokweza ya Yehova, limodzi la magawo khumi la limodzi la magawo khumi. Ndipo akuyesereninso nsembe yanu yokweza monga tirigu wa padwale, monga mopondera mphesa modzala. Momwemo inunso muzipereka kwa Yehova nsembe yokweza yochokera ku magawo anu onse a magawo khumi, a zonse muzilandira kwa ana a Israele; ndipo muperekeko nsembe yokweza ya Yehova kwa Aroni wansembe. Mupereke nsembe zokweza zonse za Yehova kuzitenga ku mphatso zanu zonse, kusankhako zokometsetsa ndizo zopatulika zake. Chifukwa chake unene nao, Pamene mukwezako zokometsetsa zake, zidzayesedwanso kwa Alevi ngati zipatso za padwale, ndi zipatso za mopondera mphesa. Ndipo muzidye pamalo ponse, inu ndi a pabanja panu; popeza ndizo mphotho yanu mwa ntchito yanu m'chihema chokomanako. Ndipo simudzasenzapo uchimo, mutakwezako zokometsetsa zake; ndipo musamaipsa zinthu zopatulika za ana a Israele, kuti mungafe. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati, Ili ndi lemba la chilamulo Yehova adalamulirachi, ndi kuti, Nena ndi ana a Israele kuti azikutengera ng'ombe yamsoti yofiira, yangwiro yopanda chilema, yosamanga m'goli; ndipo muipereke kwa Eleazara wansembe, naitulutse iye kunja kwa chigono, ndipo wina aiphe pamaso pake. Ndipo Eleazara wansembe atengeko mwazi wake ndi chala chake, nawazeko mwazi wake kasanu ndi kawiri pakhomo pa chihema chokomanako. Pamenepo atenthe ng'ombe yamsotiyo pamaso pake; atenthe chikopa chake ndi nyama yake, ndi mwazi wake, pamodzi ndi chipwidza chake. Ndipo wansembe atenge mtengo wamkungudza, ndi hisope, ndi ubweya wofiira, naziponye pakati pa moto ilikupsererapo ng'ombe yamsoti. Pamenepo wansembe atsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi; ndipo atatero alowenso kuchigono; koma wansembeyo adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo. Ndipo iye wakutentha ng'ombeyo atsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo. Ndipo munthu woyera aole mapulusa a ng'ombe yaikaziyo, nawaike kunja kwa chigono, m'malo moyera: ndipo awasungire khamu la ana a Israele akhale a madzi akusiyanitsa; ndiwo nsembe yauchimo. Ndipo wakuola mapulusayo a ng'ombe yaikazi atsuke zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; ndipo likhale lemba losatha kwa ana a Israele, ndi kwa mlendo wakukhala pakati pao. Iye wakukhudza mtembo wa munthu aliyense adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri; iyeyo adziyeretse nao tsiku lachitatu, ndi pa tsiku lachisanu ndi chiwiri adzakhala woyera; koma akapanda kudziyeretsa tsiku lachitatu, sadzakhala woyera tsiku lachisanu ndi chiwiri. Aliyense wakukhudza mtembo wa munthu aliyense wakufa, osadziyeretsa, aipsa Kachisi wa Yehova; amsadze munthuyo kwa Israele; popeza sanamwaze madzi akusiyanitsa; ndiye wodetsedwa; kudetsedwa kwake kukali pa iye. Chilamulo ndi ichi: Munthu akafa m'hema, yense wakulowa m'hemamo, ndi yense wakukhala m'hemamo, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri. Ndi zotengera zonse zovundukuka, zopanda chivundikiro chomangikapo, zili zodetsedwa. Ndipo aliyense wakukhudza munthu wophedwa ndi lupanga, kapena mtembo, kapena fupa la munthu, kapena manda, pathengo poyera, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri. Ndipo atengereko wodetsedwayo mapulusa akupsererawo a nsembe yauchimo, nathirepo m'chotengera madzi oyenda; ndi munthu woyera atenge hisope, namviike m'madzimo, ndi kuwawaza pahema ndi pa zotengera zonse, ndi pa anthu anali pomwepo, ndi pa iye wakukhudza fupa, kapena wophedwa, kapena wakufa, kapena manda. Ndipo woyerayo awaze pa wodetsedwayo tsiku lachitatu, ndi tsiku lachisanu ndi chiwiri; ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri amyeretse; ndipo atsuke zovala zake, nasambe m'madzi, nadzakhala woyera madzulo. Koma munthu wakukhala wodetsedwa, koma wosadziyeretsa, azimsadza munthuyo pakati pa msonkhano, popeza waipsa malo opatulika a Yehova; sanamwaze madzi akusiyanitsa; ndiye wodetsedwa. Ndipo likhale kwa iwo lemba losatha; kuti iye wakuwaza madzi akusiyanitsa azitsuka zovala zake; ndi iye wakukhudza madzi akusiyanitsa adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo. Ndipo chilichonse munthu wodetsedwa achikhudza chidzakhala chodetsedwa; ndi munthu wakuchikhudza adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo. Ndipo ana a Israele, ndilo khamu lonse, analowa m'chipululu cha Zini mwezi woyamba; ndipo anthu anakhala m'Kadesi; kumeneko anafa Miriyamu, naikidwa komweko. Ndipo khamulo linasowa madzi; pamenepo anasonkhana kutsutsana nao Mose ndi Aroni. Ndipo anthu anatsutsana ndi Mose, nanena, nati, Mwenzi titangomwalira muja abale athu anamwalira pamaso pa Yehova! Mwalowa nao bwanji msonkhano wa Yehova m'chipululu muno, kuti tifere mommuno, ife ndi zoweta zathu? Ndipo munatikwezeranji kutitulutsa m'Ejipito, kutilowetsa m'malo oipa ano? Si malo a mbeu awa, kapena mkuyu, kapena mpesa kapena makangaza; ngakhale madzi akumwa palibe. Ndipo Mose ndi Aroni anachoka pamaso pa msonkhano kunka ku khomo la chihema chokomanako, nagwa nkhope zao pansi; ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera iwo. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Tenga ndodoyo, nusonkhanitse khamulo; iwe ndi Aroni mbale wako, munene ndi thanthwe pamaso pao, kuti liwapatse madzi; potero uwatulutsire madzi m'thanthwe, ndi kumwetsa khamu la anthu ndi zoweta zao. Ndipo Mose anatenga ndodoyo kuichotsa pamaso pa Yehova, monga Iye anamuuza iye. Ndipo Mose ndi Aroni anasonkhanitsa msonkhano pathanthwe, nanena nao iye, Tamvanitu, opikisana naye inu; kodi tikutulutsireni madzi m'thanthwe umu? Ndipo Mose anasamula dzanja lake, napanda thanthwe kawiri ndi ndodo; ndipo madzi anatulukamo ochuluka, ndi khamulo linamwa, ndi zoweta zao zomwe. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, Popeza simunandikhulupirira Ine, kundipatula Ine pamaso pa ana a Israele, chifukwa chake simudzalowetsa msonkhano uwu m'dziko ndinawapatsali. Awa ndi madzi a Meriba; popeza ana a Israele anatsutsana ndi Yehova, ndipo anapatulidwa mwa iwowa. Pamenepo Mose anatumiza amithenga ochokera ku Kadesi kumuka kwa mfumu ya Edomu, ndi kuti, Atero mbale wanu Israele, Mudziwa zowawa zonse zinatigwera; kuti makolo athu anatsikira kunka ku Ejipito, ndipo tinakhala m'Ejipito masiku ambiri; ndipo Aejipito anachitira zoipa ife, ndi makolo athu. Pamenepo tinafuulira kwa Yehova, ndipo anamva mau athu, natuma mthenga, natitulutsa m'Ejipito; ndipo, taonani, tili m'Kadesi, ndiwo mudzi wa malekezero a malire anu. Tipitetu pakati pa dziko lanu; sitidzapitira pamunda, kapena munda wampesa, sitidzamwa madzi a m'zitsime; tidzatsata mseu wachifumu; sitidzapatukira kulamanja kapena kulamanzere, mpaka titapitirira malire anu. Koma Edomu ananena naye, Usapitire pakati pa ine, kuti ndingatuluke kukomana nawe ndi lupanga. Ndipo ana a Israele ananena naye, Tidzatsata mseu; ndipo tikakamwa madzi ako, ine ndi zoweta zanga, pamenepo ndidzapatsa mtengo wake; sindifuna kanthu kena koma kungopitapo mwa njira. Koma anati, Usapitirepo. Ndipo Edomu anatulukira kukumana naye ndi anthu ambiri, ndi dzanja lamphamvu. Potero Edomu anakana kulola Israele kupitira pa malire ake; chifukwa chake Aisraele anampatukira. Ndipo anayenda ulendo kuchokera ku Kadesi; ndi ana a Israele, ndilo khamu lonse, anadza kuphiri la Hori. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni m'phiri la Hori, pa malire a dziko la Edomu, ndi kuti, Aroni adzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wake; pakuti sadzalowa m'dziko limene ndapatsa ana a Israele, popeza munapikisana ndi mau anga ku madzi a Meriba. Tenga Aroni ndi Eleazara mwana wake, nukwere nao m'phiri la Hori; nuvule Aroni zovala zake, numveke Eleazara mwana wake; ndipo Aroni adzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wake, nadzafa komweko. Pamenepo Mose anachita monga adamulamula Yehova; ndipo anakwera m'phiri la Hori pamaso pa khamu lonse. Ndipo Mose anavula Aroni zovala zake, naveka Eleazara mwana wake; ndipo Aroni anafa pomwepo pamwamba pa phiri. Pamenepo Mose ndi Eleazara anatsika m'phirimo. Pamene khamu lonse linaona kuti Aroni adamwalira, anamlira Aroni masiku makumi atatu, ndiyo mbumba yonse ya Israele. Pamene Mkanani, mfumu ya Aradi, wokhala kumwera, anamva kuti Israele anadzera njira ya Atarimu, anathira nkhondo pa Israele, nagwira ena akhale ansinga. Ndipo Israele analonjeza chowinda kwa Yehova, nati, Mukadzaperekatu anthu awa m'dzanja langa, ndidzaononga midzi yao konse. Ndipo Yehova anamvera mau a Israele, napereka Akanani; ndipo anawaononga konse ndi midzi yao yomwe; natcha dzina lake la malowo Horoma. Ndipo anayenda ulendo kuchokera kuphiri la Hori, nadzera njira ya Nyanja Yofiira, kupaza ku dziko la Edomu; ndi mtima wa anthu unada chifukwa cha njirayo. Ndipo anthu ananena motsutsana ndi Mulungu, ndi Mose, ndi kuti, Mwatikwezeranji kutichotsa ku Ejipito kuti tifere m'chipululu? Pakuti mkate ndi madzi palibe, ndi mtima wathu walema nao mkate wachabe uwu. Pamenepo Yehova anatumiza njoka zamoto pakati pa anthu, ndipo zinaluma anthu; nafapo anthu ambiri a Israele. Ndipo anthu anadza kwa Mose, nati, Tachimwa, popeza tinanena motsutsana ndi Yehova, ndi inu; pempherani kwa Yehova kuti atichotsere njokazi. Ndipo Mose anawapempherera anthu. Pamenepo Yehova anati kwa Mose, Upange njoka yamoto, nuiike pa mtengo wake; ndipo kudzali, kuti onse olumwa, akuipenya njokayo, adzakhala ndi moyo. Ndipo Mose anapanga njoka yamkuwa, naiika pamtengo; ndipo kunali, njoka itamluma munthu aliyense, nakapenyetsetsa iye pa njoka yamkuwa, nakhala ndi moyo. Pamenepo ana a Israele anayenda ulendo, namanga mahema m'Oboti. Ndipo anachoka ku Oboti, namanga mahema ku Iyeabarimu, m'chipululu chakuno cha Mowabu, kotulukira dzuwa. Pochokapo anayenda ulendo, namanga mahema m'chigwa cha Zeredi. Atachokako anayenda ulendo, namanga mahema tsidya lina la Arinoni, wokhala m'chipululu, wogwera ku malire a Aamori; popeza Arinoni ndiwo malire a Mowabu, pakati pa Mowabu ndi Aamori. Chifukwa chake, ananena m'buku la Nkhondo za Yehova, Waheba m'Sufa, ndi miyendo ya Arinoni; ndi zigwa za miyendoyo zakutsikira kwao kwa Ari, ndi kuyandikizana ndi malire a Mowabu. Ndipo atachokapo anamuka ku Beere, ndicho chitsime chimene Yehova anachinena kwa Mose, Sonkhanitsa anthu, ndipo ndidzawapatsa madzi. Pamenepo Israele anaimba nyimbo iyi, Tumphuka chitsime iwe; muchithirire mang'ombe; chitsime adakumba mafumu, adachikonza omveka a anthu; atanena mlamuli, ndi ndodo zao. Ndipo atachoka kuchipululu anamuka ku Matana; atachoka ku Matana ku Nahaliyele; atachoka ku Nahaliyele ku Bamoti; atachoka ku Bamoti ku chigwa chili m'dziko la Mowabu, ku mutu wa Pisiga, popenyana ndi chipululu. Ndipo Israele anatuma amithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, ndi kuti, Ndipitire pakati pa dziko lako; sitidzapatuka kulowa m'munda, kapena m'munda wampesa, sitidzamwako madzi a m'zitsime; tidzatsata mseu wachifumu, kufikira tapitirira malire ako. Ndipo Sihoni sanalole Israele apitire m'malire ake; koma Sihoni anamemeza anthu ake onse, nadzakomana naye Israele m'chipululu, nafika ku Yahazi, nathira nkhondo pa Israele. Ndipo Israele anamkantha ndi lupanga lakuthwa, nalanda dziko lake likhale laolao, kuyambira Arinoni kufikira Yaboki, kufikira ana a Amoni; popeza malire a ana a Amoni ndiwo olimba. Ndipo Israele analanda midzi iyi yonse; nakhala Israele m'midzi yonse ya Aamori; m'Hesiboni ndi milaga yake yonse. Popeza Hesiboni ndiwo mudzi wa Sihoni mfumu ya Aamori, imene idathira nkhondo pa mfumu idafayo ya Mowabu, nilanda dziko lake m'dzanja lake kufikira Arinoni. Chifukwa chake iwo akunena mophiphiritsa akuti, Idzani ku Hesiboni, mudzi wa Sihoni umangike, nukhazikike. Popeza moto unatuluka m'Hesiboni, chirangali cha moto m'mudzi wa Sihoni; chatha Ari wa Mowabu, eni misanje ya Arinoni. Tsoka kwa iwe, Mowabu! Mwaonongeka, anthu a Kemosi inu, anapereka ana ake amuna opulumuka, ndi ana ake akazi akhale ansinga, kwa Sihoni mfumu ya Aamori. Tinawagwetsa; Hesiboni waonongeka kufikira ku Diboni, ndipo tinawapululutsa kufikira ku Nofa. Ndiwo wakufikira ku Medeba. Chomwecho Israele anakhala m'dziko la Aamori. Ndipo Mose anatumiza anthu akazonde Yazere, nalanda milaga yake, napirikitsa Aamori a komweko. Ndipo anatembenuka nakwera kudzera njira ya ku Basani; ndipo Ogi mfumu ya ku Basani anatuluka kukumana nao, iye ndi anthu ake onse, kudzachita nao nkhondo ku Ederei. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Usamuopa; popeza ndampereka m'manja mwako, iye ndi anthu ake onse, ndi dziko lake; umchitire monga umo unachitira Sihoni mfumu ya Aamori anakhalayo ku Hesiboni. Ndipo anamkantha iye, ndi ana ake amuna ndi anthu ake onse, kufikira sanatsale ndi mmodzi yense; nalanda dziko lake likhale laolao. Ndipo ana a Israele anayenda ulendo, namanga mahema m'zigwa za Mowabu, tsidya la Yordani ku Yeriko. Ndipo Balaki mwana wa Zipori anaona zonse Israele anachitira Aamori. Ndipo Mowabu anachita mantha akulu ndi anthuwo, popeza anachuluka; nada mtima Mowabu chifukwa cha ana a Israele. Ndipo Mowabu anati kwa akulu a Midiyani, Tsopano msonkhano uwu udzanyambita zonse zili pozinga pathu, monga ng'ombe zinyambita msipu wa kubusa. Ndipo Balaki mwana wa Zipori anali mfumu ya Mowabu masiku amenewo. Ndipo anatuma amithenga kwa Balamu mwana wa Beori, ku Petori, wokhala kumtsinje, wa dziko la anthu a mtundu wake, kuti amuitane, ndi kuti, Taonani, anatuluka anthu m'dziko la Ejipito; taonani, aphimba nkhope ya dziko, nakhala popenyana ndi ine. Ndipo tsopano, idzatu, nunditembererere anthu awa; popeza andiposa mphamvu; kapena ndidzawapambana, kuti tiwakanthe, ndi kuti ndiwapirikitse m'dziko; pakuti ndidziwa kuti iye amene umdalitsa adalitsika, ndi iye amene umtemberera atemberereka. Ndipo akulu a Mowabu ndi akulu a Midiyani anamuka ndi mphotho za maula m'dzanja lao; anadza kwa Balamu, nanena naye mau a Balaki. Ndipo ananena nao, Mugone kuno usiku uno, ndidzakubwezerani mau, monga Yehova adzanena ndi ine; pamenepo mafumu a Mowabu anagona ndi Balamu. Ndipo Mulungu anadza kwa Balamu, nati, Anthu awa ali ndi iwe ndiwo ayani? Ndipo Balamu anati kwa Mulungu, Balaki mwana wa Zipori mfumu ya Mowabu, anatumiza kwa ine, ndi kuti, Taonani, anthu awa adatuluka m'Ejipito aphimba nkhope ya dziko, idzatu unditembererere awa; kapena ndidzakhoza kulimbana nao nkhondo, ndi kuwapirikitsa. Koma Mulungu anati kwa Balamu, Usapita nao; usatemberera anthuwa; pakuti adalitsika. Ndipo Balamu anauka m'mawa, nati kwa akalonga a Balaki, Mukani ku dziko lanu; popeza Yehova andikaniza kuti ndisapite nanu. Pamenepo akalonga a Mowabu ananyamuka, nafika kwa Balaki, nati Alikukana Balamu kudza nafe. Koma Balaki anaonjeza kutumanso akalonga, ochuluka, ndi omveka koposa awa. Ndipo anadza kwa Balamu, nati kwa iye, Atero Balaki mwana wa Zipori, Pasakhaletu chinthu chakukuletsa kudza kwa ine; popeza ndidzakuchitira ulemu waukulu, ndipo zonse unena ndi ine ndidzachita; chifukwa chake idzatu, unditembererere anthu awa. Ndipo Balamu anayankha nati kwa anyamata a Balaki, Chinkana Balaki andipatsa nyumba yake yodzala ndi siliva ndi golide, sindikhoza kutumpha mau a Yehova Mulungu wanga, kuchepsako kapena kuonjezako. Ndikupemphani, tsono, khalani pano inu usiku uno womwe; kuti ndidziwe chomwe Yehova adzanenanso nane. Ndipo Mulungu anadza kwa Balamu usiku, nanena naye, Akadza kukuitana anthuwa, nyamuka, kunka nao, koma mau okhaokha ndinena ndi iwe, ndiwo ukachite. Pamenepo Balamu anauka m'mawa namanga bulu wake, namuka nao akalonga a ku Mowabu. Koma anapsa mtima Mulungu chifukwa cha kupita iye, ndipo mthenga wa Yehova anadziika m'njira wotsutsana naye. Ndipo anali wokwera pa bulu wake, ndi anyamata ake awiri anali naye. Ndipo buluyo anaona mthenga wa Yehova alikuima m'njira, ndi lupanga lake ku dzanja lake; ndi bulu anapatuka m'njira, nalowa kuthengo; ndipo Balamu anampanda bulu kumbwezera kunjira. Pamenepo mthenga wa Yehova anaima m'njira yopapatiza ya minda yampesa; mbali ina kuli linga, mbali ina linga. Ndipo bulu anaona mthenga wa Yehova, nadzikankhira kulinga, nakanikiza phazi la Balamu kulinga; ndipo anampandanso. Pamenepo mthenga wa Yehova anapitiriranso, naima popapatiza, popanda popatukira kulamanja kapena kulamanzere. Ndipo bulu wake anaona mthenga wa Yehova, nagona pansi, Balamu ali pamsana pake; ndipo Balamu adapsa mtima, nampanda bulu ndi ndodo. Ndipo Yehova anatsegula pakamwa pake pa bulu, nati uyu kwa Balamu, Ndakuchitanji, kuti wandipanda katatu tsopano? Pamenepo Balamu anati kwa bulu, Chifukwa wandipeputsa; mukadakhala lupanga m'dzanja langa tsopano, ndikadakupha iwe. Ndipo bulu anati kwa Balamu, Si ndine bulu wako amene umayenda wokwera pa ine chiyambire ndili wako kufikira lero lino? Kodi ndikakuchitira chotere ndi kale lonse? Ndipo anati, Iai. Pamenepo Yehova anapenyetsa maso a Balamu, naona iye mthenga wa Yehova alikuima m'njira, lupanga losolola lili kudzanja, ndipo anawerama mutu wake, nagwa nkhope yake pansi. Ndipo mthenga wa Yehova ananena naye, Wapandiranji bulu wako katatu tsopano? Taona, ndatuluka kuti nditsutsane nawe popeza njira iyi ikugwetsa chamtu pamaso panga; koma bulu anandiona, nandipatukira nthawi izi zitatu pondiona; akadapanda kundipatukira, ndikadakupha iwe ndithu, ndi kumsunga iye wamoyo. Pamenepo Balamu anati kwa mthenga wa Yehova, Ndachimwa, popeza sindinadziwa kuti munaima mondiletsa m'njira; ndipo tsopano, ngati chikuipirani, ndibwerera. Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa Balamu, Pita nao anthuwa; koma mau okhaokha ndinena ndi iwe, ndiwo ukanene. Potero Balamu anamuka nao akalonga a Balaki. Pamene Balaki anamva kuti wafika Balamu, anamtulukira kukakomana naye kumudzi wa Mowabu, wokhala m'mphepete mwa Arinoni, ndiwo ku malekezero a malire ake. Ndipo Balaki anati kwa Balamu, Kodi sindinatumiza kwa iwe ndithu kukakuitana? Unalekeranji kudza kwa ine? Sindikhoza kodi kukuchitira ulemu? Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Taonani, ndafika kwa inu; ngati ndili nayo mphamvu konse tsopano kunena kanthu? Mau amene Mulungu aike m'kamwa mwanga ndiwo ndidzanena. Ndipo Balamu anamuka ndi Balaki, nafika iwo ku Kiriyati-Huzoti. Pamenepo Balaki anapha ng'ombe ndi nkhosa, natumizira Balamu, ndi akalonga okhala naye. Ndipo kunali kuti m'mawa, Balaki anatenga Balamu, nakwera naye ku misanje ya Baala, ndi kumeneko anaona malekezero a anthuwo. Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Ndimangireni kuno maguwa a nsembe asanu ndi awiri, nimundikonzere kuno ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri. Ndipo Balaki anachita monga Balamu ananena; ndipo Balaki ndi Balamu anapereka pa guwa la nsembe lililonse ng'ombe ndi nkhosa yamphongo. Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Imani pa nsembe yopsereza yanu, ndipite ine, kapena Yehova akadza kukomana ndi ine; ndipo chimene akandionetsa ine ndidzakufotokozerani. Ndipo anapita pamsanje poyera. Pamenepo Mulungu anakomana ndi Balamu; ndipo ananena ndi iye, Ndakonza maguwa a nsembe asanu ndi awiri, ndipo ndapereka ng'ombe ndi nkhosa yamphongo pa guwa la nsembe lililonse. Ndipo Yehova anaika mau m'kamwa mwa Balamu, nati, Bwerera kwa Balaki, nukanene chakutichakuti. Ndipo anabwerera kwa iye, ndipo, taonani, analikuima pa nsembe yopsereza yake, iye ndi akalonga onse a Mowabu. Ndipo ananena fanizo lake, nati, Ku Aramu ananditenga Balaki, mfumu ya Mowabu ananditenga ku mapiri a kum'mawa, Idza, udzanditembererere Yakobo. Idza, nudzanyoze Israele. Ndidzatemberera bwanji amene Mulungu sanamtemberere? Ndidzanyoza bwanji, amene Yehova sanamnyoze? Pakuti, pokhala pamwamba pa matanthwe ndimpenya, pokhala pa zitunda ndimuyang'ana; taonani, ndiwo anthu akukhala pa okha. Osadziwerengera pakati pa amitundu ena. Adzawerenga ndani fumbi la Yakobo, kapena kuwerenga limodzi la magawo anai la Israele? Ndipo ine ndife monga amafa oongoka mtima, chitsiriziro changa chifanane nacho chake! Pamenepo Balaki anati kwa Balamu, Wandichitiranji? Ndinakutenga utemberere adani anga, ndipo taona, wawadalitsa ndithu. Ndipo anayankha nati, Chimene achiika m'kamwa mwanga Yehova, sindiyenera kodi kunena ichi? Ndipo Balaki anati naye, Tiyetu, upite nane kumalo kwina, kumene ukawaona; udzaona malekezero ao okha, osawaona onse; ndipo pokhala pamenepo ukanditembererere iwo. Ndipo anamuka naye ku thengo la Zofimu, pamwamba pa Pisiga, namangako maguwa a nsembe asanu ndi awiri, napereka ng'ombe ndi nkhosa yamphongo pa guwa la nsembe lililonse. Ndipo anati kwa Balaki, Imani pano pa nsembe yopsereza yanu, ndipite ine ndikakomane ndi Iye uko. Ndipo Yehova anakomana naye Balamu, naika mau m'kamwa mwake, nati, Bwerera kwa Balaki, nukanene chakutichakuti. Ndipo anadza kuli iye, ndipo taona, analikuima pa nsembe yake yopsereza, ndi akalonga a Mowabu pamodzi naye. Ndipo Balaki anati kwa iye, Wanenanji Yehova? Ndipo ananena fanizo lake, nati, Ukani, Balaki, imvani; ndimvereni, mwana wa Zipori. Mulungu sindiye munthu, kuti aname; kapena mwana wa munthu, kuti aleke; kodi anena, osachita? Kapena kulankhula, osachitsimikiza? Taonani, ndalandira mau akudalitsa, popeza Iye wadalitsa, sinditha kusintha. Sayang'anira mphulupulu ili m'Yakobo, kapena sapenya kupulukira kuli m'Israele. Yehova Mulungu wake ali ndi iye, ndi mfuu wa mfumu uli pakati pao. Mulungu awatulutsa m'Ejipito; mphamvu yake ikunga ya njati. Pakuti palibe nyanga pakati pa Yakobo, kapena ula mwa Israele; pa nyengo yake adzanena kwa Yakobo ndi Israele, chimene Mulungu achita. Taonani, anthuwo auka ngati mkango waukazi, nadzitukumula ngati mkango waumuna. Sugonanso kufikira utadya nyama yogwira, utamwa mwazi wa zophedwa. Ndipo Balaki anati kwa Balamu, Usawatemberera konse, kapena kuwadalitsa konse. Koma Balamu anayankha nati kwa Balaki, Sindinakuuzani ndi kuti, Chilichonse achinena Yehova, chomwecho ndizichita? Ndipo Balaki anati kwa Balamu, Tiyetu, ndimuke nawe kumalo kwina; kapena kudzakomera pamaso pa Mulungu kuti unditembererere iwo pokhala kumeneko. Ndipo Balaki ananka naye Balamu pamwamba pa Peori, popenyana ndi chipululu. Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Mundimangire pano maguwa a nsembe asanu ndi awiri, nimundikonzere pano ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri. Ndipo Balaki anachita monga adanena Balamu, napereka ng'ombe ndi nkhosa yamphongo pa guwa la nsembe lililonse. Pamene Balamu anaona kuti kudakomera pamaso pa Yehova kudalitsa Israele, sanamuke, monga nthawi zija zina, ku nyanga zolodzera, koma anayang'ana nkhope yake kuchipululu. Ndipo Balamu anakweza maso ake, naona Israele alikukhala monga mwa mafuko ao; ndipo mzimu wa Mulungu unadza pa iye. Pamenepo ananena fanizo lake, nati, Balamu mwana wa Beori anenetsa, ndi munthuyo anatsinzina maso anenetsa; anenetsa wakumva mau a Mulungu, wakuona masomphenya a Wamphamvuyonse, wakugwa pansi maso ake openyuka. Ha? Mahema ako ngokoma, Yakobo; zokhalamo zako, Israele! Ziyalika monga zigwa, monga minda m'mphepete mwa nyanja, monga khonje wooka Yehova, monga mikungudza m'mphepete mwa madzi. Madzi adzayenda natuluka m'zotungira zake, ndi mbeu zake zidzakhala ku madzi ambiri, ndi mfumu yake idzamveka koposa Agagi, ndi ufumu wake udzamveketsa. Mulungu amtulutsa m'Ejipito; ali nayo mphamvu yonga ya njati; adzawadya amitundu, ndiwo adani ake. Nadzamphwanya mafupa ao, ndi kuwapyoza ndi mivi yake. Anauthama, nagona pansi ngati mkango, ngati mkango waukazi; adzamuutsa ndani? Wodalitsika aliyense wakudalitsa iwe, wotemberereka aliyense wakutemberera iwe. Pamenepo Balaki anapsa mtima pa Balamu, naomba m'manja; ndipo Balaki anati kwa Balamu, Ndinakuitana kutemberera adani anga, ndipo unawadalitsa ndithu katatu tsopano. Chifukwa chake thawira ku malo ako tsopano; ndikadakuchitira ulemu waukulu; koma, taona, Yehova wakuletsera ulemu. Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Kodi sindinauzanso amithenga anu amene munawatumiza kwa ine, ndi kuti, Chinkana Balaki akandipatsa nyumba yake yodzala ndi siliva ndi golide, sindikhoza kutumpha mau a Yehova, kuchita chokoma kapena choipa ine mwini wake; chonena Yehova ndicho ndidzanena ine? Ndipo tsopano, taonani, ndimuka kwa anthu a mtundu wanga; tiyeni, ndidzakulangizani, ndi kukuuzani zimene anthu awa adzachitira anthu anu, masiku otsiriza. Ndipo ananena fanizo lake, nati, Balamu mwana wa Beori anenetsa, ndi munthu wotsinzina masoyo anenetsa; anenetsa wakumva mau a Mulungu, ndi kudziwa nzeru ya Wam'mwambamwamba, wakuona masomphenya a Wamphamvuyonse, wakugwa pansi wopenyuka maso. Ndimuona, koma tsopano ai; ndimpenya, koma si pafupi ai; idzatuluka nyenyezi m'Yakobo, ndi ndodo yachifumu idzauka m'Israele, nidzakantha malire a Mowabu, nidzapasula ana onse a Seti. Ndi Edomu adzakhala akeake, Seiri lomwe lidzakhala lakelake, ndiwo adani ake; koma Israele adzachita zamphamvu. Ndipo wina wotuluka m'Yakobo adzachita ufumu; nadzapasula otsalira m'mudzi. Ndipo anayang'ana ku Amaleke, nanena fanizo lake, nati, Amaleke ndiye woyamba wa amitundu; koma chitsiriziro chake, adzaonongeka ku nthawi zonse. Ndipo anayang'ana Akeni, nanena fanizo lake, nati, kwanu nkokhazikika, wamanga chisa chako m'thanthwe. Koma Kaini adzaonongeka, kufikira Asiriya adzakumanga nsinga. Ndipo ananena fanizo lake, nati, Ha! Adzakhala ndi moyo ndani pakuchita ichi Mulungu? Koma zombo zidzafika kuchokera ku dooko la Kitimu, ndipo adzasautsa Asiriya, nadzasautsa Eberi, koma iyenso adzaonongeka. Ndipo Balamu anauka, namuka nabwerera kumalo kwake; ndi Balaki yemwe ananka njira yake. Ndipo Israele anakhala m'Sitimu, ndipo anthu anayamba kuchita chigololo ndi ana akazi a Mowabu; popeza anaitana anthuwo adze ku nsembe za milungu yao; ndipo anthuwo anadya, nagwadira milungu yao. Pamene Israele anaphatikana ndi Baala-Peori, Yehova anapsa mtima pa Israele. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Gwira akulu onse a anthu nuwapachikire Yehova, pali dzuwa poyera, kuti mkwiyo waukali wa Yehova uchoke kwa Israele. Ndipo Mose anati kwa oweruza a Israele, Iphani, yense anthu ake adaphatikanawo ndi Baala-Peori. Ndipo, taonani, anadza wina wa ana a Israele, nabwera naye mkazi Mmidiyani kudza naye kwa abale ake, pamaso pa Mose, ndi pamaso pa khamu lonse la ana a Israele, pakulira iwo pa khomo la chihema chokomanako. Pamene Finehasi mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, anachiona, anauka pakati pa khamu, natenga nthungo m'dzanja lake; natsata munthu Mwisraele m'hema, nawamoza onse awiri, munthu Mwisraele ndi mkaziyo m'mimba mwake. Pamenepo mliri unaletseka kwa ana a Israele. Ndipo akufa nao mliri ndiwo zikwi makumi awiri ndi zinai. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Finehasi mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, wabweza kuzaza kwanga pa ana a Israele, popeza anachita nsanje ndi nsanje yanga pakati pao, kotero kuti sindinawatha ana a Israele m'nsanje yanga. Chifukwa chake nena, Taonani, ndimpatsa iye pangano langa la mtendere; ndipo lidzakhala kwa iye, ndi kwa mbeu zake zakumtsata pangano la unsembe wosatha, popeza anachita nsanje chifukwa cha Mulungu wake, anawachitira ana a Israele chowatetezera. Koma dzina la Mwisraele adamuphayo, ndiye amene adamupha pamodzi ndi mkazi Mmidiyani, ndiye Zimiri mwana wa Salu, mfumu ya nyumba ya makolo mwa Asimeoni. Ndi dzina la mkazi Mmidiyani adamuphayo ndiye Kozibi mwana wamkazi wa Zuri; ndiye mkulu wa anthu a nyumba ya makolo m'Midiyani. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Sautsa Amidiyani ndi kuwakantha; popeza akusautsani ndi manyengo ao amene anakunyengani nao; m'chija cha Peori, ndi cha Kozibi, mwana wamkazi wa kalonga wa ku Midiyani, mlongo wao, amene adamupha tsiku la mliri, m'chija cha Peori. Ndipo kunali, utatha mliriwo, Yehova ananena ndi Mose ndi Eleazara mwana wa Aroni wansembe, nati, Werenga khamu lonse la ana a Israele, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, monga mwa nyumba za makolo ao, onse akutulukira kunkhondo m'Israele. Pamenepo Mose ndi Eleazara wansembe ananena nao m'zidikha za Mowabu pa Yordani kufupi ku Yeriko, ndi kuti, Awawerenge kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu; monga Yehova anawauza Mose ndi ana a Israele, amene adatuluka m'dziko la Ejipito. Rubeni, ndiye woyamba kubadwa wa Israele; ana amuna a Rubeni ndiwo: Hanoki, ndiye kholo la banja la Ahanoki; Palu, ndiye kholo la banja la Apalu; Hezironi, ndiye kholo la banja la Ahezironi; Karimi, ndiye kholo la banja la Akarimi. Iwo ndiwo mabanja a Arubeni; owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu. Mwana wamwamuna wa Palu ndiye Eliyabu. Ndi ana a Eliyabu: Nemuwele, ndi Datani ndi Abiramu. Iwo ndiwo Datani ndi Abiramu omwe aja oitanidwa a khamu, amene anatsutsana ndi Mose ndi Aroni mu msonkhano wa Kora, muja anatsutsana ndi Yehova; ndipo dziko linayasama pakamwa pake, ndi kuwameza pamodzi ndi Kora, pakufa msonkhano uja; muja moto unaononga amuna mazana awiri ndi makumi asanu, nakhala iwo chizindikiro. Koma sanafe ana amuna a Kora. Ana amuna a Simeoni monga mwa mabanja ao ndiwo: Nemuwele, ndiye kholo la banja la Anemuwele; Yamini, ndiye kholo la banja la Ayamini; Yakini, ndiye kholo la banja la Ayakini; Zera, ndiye kholo la banja la Azera; Shaulo, ndiye kholo la banja la Ashaulo. Iwo ndiwo mabanja a Asimeoni, zikwi makumi awiri mphambu ziwiri kudza mazana ziwiri. Ana amuna a Gadi monga mwa mabanja ao ndiwo: Zefoni, ndiye kholo la banja la Azefoni; Hagi, ndiye kholo la banja la Ahagi; Suni, ndiye kholo la banja la Suni; Ozini, ndiye kholo la banja la Aozini; Eri, ndiye kholo la banja la Aeri; Arodi, ndiye kholo la banja la Aarodi; Areli, ndiye kholo la banja la Aareli. Iwo ndiwo mabanja a ana a Gadi, monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi anai ndi mazana asanu. Ana amuna a Yuda, ndiwo Eri ndi Onani; ndipo Eri ndi Onani anamwalira m'dziko la Kanani. Ndipo ana a Yuda monga mwa mabanja ao ndiwo: Sela, ndiye kholo la banja la Asela; Perezi, ndiye kholo la banja la Aperezi; Zera, ndiye kholo la banja la Azera. Ndipo ana a Perezi ndiwo: Hezironi, ndiye kholo la banja la Ahezironi; Hamuli, ndiye kholo la banja la Ahamuli. Iwo ndiwo mabanja a Yuda monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi kudza mazana asanu. Ana amuna a Isakara monga mwa mabanja ao ndiwo: Tola, ndiye kholo la banja la Atola; Puva, ndiye kholo la banja la Apuni; Yasubu, ndiye kholo la banja la Ayasubu; Simironi, ndiye kholo la banja la Asimironi. Iwo ndiwo mabanja a Isakara monga mwa owerengedwa ao; zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu zinai kudza mazana atatu. Ana amuna a Zebuloni monga mwa mabanja ao ndiwo: Seredi, ndiye kholo la banja la Aseredi; Eloni, ndiye kholo la banja la Aeloni; Yaleele, ndiye kholo la banja la Ayaleele. Iwo ndiwo mabanja a Zebuloni monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu mazana asanu. Ana amuna a Yosefe monga mwa mabanja ao ndiwo: Manase ndi Efuremu. Ana a Manase ndiwo: Makiri, ndiye kholo la banja la Amakiri; ndipo Makiri anabala Giliyadi; ndiye kholo la banja la Agiliyadi. Ana a Giliyadi ndiwo: Iyezere, ndiye kholo la banja la Aiyezere; Heleki, ndiye kholo la banja la Aheleki; ndi Asiriele, ndiye kholo la banja la Aasiriele; ndi Sekemu, ndiye kholo la banja la Asekemu; ndi Semida, ndiye kholo la banja la Asemida; ndi Hefere, ndiye kholo la banja la Ahefere. Ndipo Zelofehadi mwana wa Hefere analibe ana amuna, koma ana akazi ndiwo; ndipo maina a ana akazi a Tselofekadi ndiwo Mala ndi Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza. Iwo ndiwo mabanja ao a Manase; ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi asanu mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi awiri. Ana amuna a Efuremu monga mwa mabanja ao ndiwo: Sutela, ndiye kholo la banja la Asutela; Bekere, ndiye kholo la banja la Abekere; Tahani, ndiye kholo la banja la Atahani. Ndipo mwana wamwamuna wa Sutela ndiye Erani, ndiye kholo la banja la Aerani. Iwo ndiwo mabanja a ana a Efuremu monga mwa owerengedwa ao, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu ziwiri kudza mazana asanu. Iwo ndiwo ana amuna a Yosefe monga mwa mabanja ao. Ana amuna a Benjamini monga mwa mabanja ao ndiwo: Bela, ndiye kholo la banja la Abela; Asibele, ndiye kholo la banja la Aasibele; Ahiramu, ndiye kholo la banja la Aahiramu; Sefufamu ndiye kholo la banja la Asefufamu; Hufamu, ndiye kholo la banja la Ahufamu. Ndipo ana amuna a Bela ndiwo Aridi ndi Naamani; Aridi, ndiye kholo la banja la Aaridi; Naamani, ndiye kholo la banja la Anaamani. Iwo ndiwo ana a Benjamini monga mwa mabanja ao; ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana asanu ndi limodzi. Mwana wamwamuna wa Dani monga mwa mabanja ake ndiye Suhamu, ndiye kholo la banja la Asuhamu. Iwo ndiwo mabanja a Dani monga mwa mabanja ao. Mabanja onse a Asuhamu monga mwa owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu zinai kudza mazana anai. Ana amuna a Asere monga mwa mabanja ao ndiwo: Imina, ndiye kholo la banja la Imina; Isivi, ndiye kholo la banja la Aisivi; Beriya, ndiye kholo la banja la Aberiya. Ana a Beriya ndiwo: Hebere, ndiye kholo la banja la Ahebere; Malikiele, ndiye kholo la banja la Amalikiele. Ndipo dzina la mwana wamkazi wa Asere ndiye Sera. Iwo ndiwo mabanja a ana amuna a Asere monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi asanu mphambu zitatu kudza mazana anai. Ana amuna a Nafutali monga mwa mabanja ao ndiwo: Yazeele, ndiye kholo la banja la Ayezeele; Guni, ndiye kholo la banja la Aguni; Yezere, ndiye kholo la banja la Ayezere; Silemu, ndiye kholo la banja la Asilemu. Iwo ndiwo mabanja a Nafutali, monga mwa mabanja ao; ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana anai. Iwo ndiwo owerengedwa ao a ana a Israele, zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu chimodzi kudza mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Dziko ligawikire iwowa monga mwa kuwerenga kwa maina, likhale cholowa chao. Ochulukawo, uwachulukitsire cholowa chao; ochepawo uwachepetsere cholowa chao; ampatse yense cholowa chake monga mwa owerengedwa ake. Koma aligawe ndi kuchita maere; cholowa chao chikhale monga mwa maina a mafuko a makolo ao. Agawire ochuluka ndi ochepa cholowa chao monga mwa kuchita maere. Ndipo awa ndi owerengedwa ao a Alevi monga mwa mabanja ao: Geresoni, ndiye kholo la banja la Ageresoni; Kohati, ndiye kholo la banja la Akohati; Merari, ndiye kholo la banja la Amerari. Awa ndi mabanja a Alevi: banja la Alibini, banja la Ahebroni, banja la Amali, banja la Amusi, banja la Akora. Ndipo Kohati anabala Amuramu. Ndipo dzina lake la mkazi wake wa Amuramu ndiye Yokebede, mwana wamkazi wa Levi, wobadwira Levi m'Ejipito; ndipo iye anambalira Amuramu, Aroni ndi Mose, ndi Miriyamu mlongo wao. Ndipo Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara anabadwira Aroni. Koma Nadabu ndi Abihu adafa, muja anabwera nao moto wachilendo pamaso pa Yehova. Ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi awiri mphambu zitatu, mwamuna yense wa mwezi umodzi ndi mphambu; popeza sanawerengedwe pakati pa ana a Israele; chifukwa sanawapatse cholowa mwa ana a Israele. Iwo ndiwo amene anawerengedwa ndi Mose ndi Eleazara wansembe, amene anawerenga ana a Israele m'zidikha za Mowabu ku Yordani pafupi pa Yeriko. Koma pakati pao panalibe mmodzi wa iwo amene anawerengedwa ndi Mose ndi Aroni wansembe, amene anawerenga ana a Israele m'chipululu cha Sinai. Popeza Yehova adanena za iwowa, Adzafatu m'chipululu. Ndipo sanatsalire mmodzi wa iwowa koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni. Pamenepo anayandikiza ana akazi a Zelofehadi mwana wa Hefere, ndiye mwana wa Giliyadi, ndiye mwana wa Makiri, ndiye mwana wamwamuna wa Manase, wa mabanja a Manase mwana wa Yosefe; ndipo maina a ana ake akazi ndiwo, Mala, Nowa, Hogila ndi Milika ndi Tiriza. Ndipo anaima pamaso pa Mose, ndi pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa akalonga; ndi khamu lonse, pakhomo pa chihema chokomanako, ndi kuti, Atate wathu adamwalira m'chipululu, ndipo sanakhale iye pakati pa msonkhano wa iwo akusonkhana kutsutsana ndi Yehova, mu msonkhano wa Kora; koma anafera zoipa zakezake; ndipo analibe ana amuna. Lichotsedwerenji dzina la atate wathu pakati pa banja lake, popeza alibe mwana wamwamuna? Tipatseni dziko lathulathu pakati pa abale a atate wathu. Ndipo Mose anapita nao mlandu wao pamaso pa Yehova. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Ana akazi a Zelofehadi anena zoona; uwapatse ndithu cholowa chikhale chaochao pakati pa abale a atate wao; nuwalandiritse cholowa cha atate wao. Ndipo unene ndi ana a Israele, ndi kuti, Akafa munthu wamwamuna wopanda mwana wamwamuna, cholowa chake achilandire mwana wake wamkazi. Ndipo akapanda kukhala naye mwana wamkazi, mupatse abale ake cholowa chake. Ndipo akapanda kukhala nao abale, mupatse abale a atate wake cholowa chake. Ndipo akapanda abale a atate wake, mupatse wa chibale chake woyandikizana naye wa fuko lake cholowa chake, likhale lakelake; ndipo likhale kwa ana a Israele lemba monga Yehova wamuuza Mose. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Kwera m'phiri ili la Abarimu, nupenye dziko limene ndapatsa ana a Israele. Utaliona iwenso udzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wako, monga anaitanidwa Aroni mbale wako; popeza munapikisana nao mau anga m'chipululu cha Zini, potsutsana nane khamulo, osandipatula Ine pa madziwo pamaso pao. Ndiwo madzi a Meriba m'Kadesi, m'chipululu cha Zini. Ndipo Mose ananena ndi Yehova, nati, Yehova, Mulungu wa mizimu ya anthu onse, aike munthu pa khamulo, wakutuluka pamaso pao, ndi kulowa pamaso pao, wakuwatulutsa ndi kuwalowetsa; kuti khamu la Ambuye lisakhale ngati nkhosa zopanda mbusa. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Utenge Yoswa mwana wa Nuni, ndiye munthu mwa iye muli mzimu, nuike dzanja lako pa iye; numuimike pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa khamu lonse; numlangize pamaso pao. Ndipo umuikirepo ulemerero wako, kuti khamu lonse la ana a Israele ammvere. Ndipo aime pamaso pa Eleazara wansembe, amene amfunsire monga mwa chiweruzo cha Urimu pamaso pa Yehova; ponena iye azituluka, ndi ponena iye azilowa, ndi iye ndi ana onse a Israele pamodzi naye, ndiwo khamu lonse. Ndipo Mose anachita monga Yehova adamuuza; natenga Yoswa namuimitsa pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa khamu lonse; namuikira manja ake, namlangiza monga Yehova adanena ndi dzanja la Mose. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Uza ana a Israele, nuti nao, Muzisamalira kubwera nacho kwa Ine chopereka changa, chakudya changa cha nsembe zanga zamoto, cha fungo lokoma, pa nyengo yake yoikika. Ndipo unene nao, Nsembe yamoto imene muzibwera nayo kwa Yehova ndiyi: anaankhosa awiri a chaka chimodzi opanda chilema, tsiku ndi tsiku, nsembe yamoto yosalekeza. Mwanawankhosa mmodziyo umpereke m'mawa, ndi mwanawankhosa winayo umpereke madzulo; ndi limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wosalala ukhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi limodzi la magawo anai la hini wa mafuta opera. Ndiyo nsembe yopsereza kosalekeza, yoikika kuphiri la Sinai, ichite fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova. Ndi nsembe yake yothira ya mwanawankhosa mmodziyo ndiyo limodzi la magawo anai la hini; m'malo opatulika uthirire Yehova nsembe yothira ya chakumwa cholimba. Ndi mwanawankhosa winayo umpereke madzulo; monga nsembe yaufa ya m'mawa, ndi nsembe yothira yake, umpereke; ndiyo nsembe yamoto ya fungo lokoma la Yehova. Ndipo tsiku la Sabata anaankhosa awiri a chaka chimodzi, opanda chilema, ndi awiri a magawo khumi a efa wa ufa wosalala, ukhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndi nsembe yake yothira; ndiyo nsembe yopsereza ya tsiku la Sabata lililonse, pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yothira. Ndipo poyamba miyezi yanu muzibwera nayo nsembe yopsereza ya Yehova: ng'ombe zamphongo ziwiri, ndi nkhosa yamphongo imodzi, ndi anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi opanda chilema; ndi atatu a magawo khumi a efa wa ufa wosalala, ikhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndiwo wa ng'ombe iliyonse; ndi awiri a magawo khumi a ufa wosalala, ikhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndiwo wa nkhosa yamphongo imodziyo; ndi limodzi la magawo khumi la ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa, ndiwo wa mwanawankhosa yense; ndiyo nsembe yopsereza ya fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova. Ndipo nsembe zake zothira ndizo: limodzi la magawo khumi la hini wa vinyo ndiwo wa ng'ombe imodzi, ndi limodzi la magawo atatu la hini likhale la nkhosa yamphongo, ndi limodzi la magawo anai a hini likhale la mwanawankhosa; ndiyo nsembe yopsereza ya mwezi uliwonse kunena miyezi yonse ya chaka. Ndi tonde mmodzi, akhale nsembe yauchimo ya Yehova; aikonze pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yothira. Ndipo mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi pali Paska wa Yehova. Ndipo tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi uwu pali zikondwerero; masiku asanu ndi awiri azidya mkate wopanda chotupitsa. Tsiku loyamba pali kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena; koma mubwere nayo nsembe yamoto, nsembe yopsereza ya Yehova; ng'ombe ziwiri zamphongo, ndi nkhosa yamphongo imodzi, ndi anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi; akhale kwa inu opanda chilema; ndi nsembe yao ya efa wa ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta; mupereke atatu a magawo khumi akhale a ng'ombe, ndi awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo; upereke limodzi la magawo khumi likhale la mwanawankhosa mmodzi; uzitero ndi anaankhosa asanu ndi awiri; ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo, yakutetezera inu. Mupereke izi pamodzi ndi nsembe yopsereza ya m'mawa, ndiyo ya nsembe yopsereza kosalekeza. Momwemo mupereke chakudya cha nsembe yamoto cha fungo lokoma la Yehova, tsiku ndi tsiku, masiku asanu ndi awiri, chakupereka pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yothira. Ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri mukhale nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena. Momwemonso tsiku la zipatso zoyamba, pobwera nayo nsembe ya ufa watsopano kwa Yehova, m'chikondwerero chanu cha Masabata, muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena. Pamenepo muzipereka nsembe yopsereza ya fungo lokoma kwa Yehova; ng'ombe zamphongo ziwiri, nkhosa yamphongo imodzi, anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi; ndi nsembe yake ya efa wa ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a ng'ombe imodzi, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo imodzi, limodzi la magawo khumi likhale la mwanawankhosa mmodzi, momwemo ndi anaankhosa asanu ndi awiri; tonde mmodzi wakutetezera inu. Mupereke izi pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, zikhale kwa inu zopanda chilema, ndi nsembe zake zothira. Ndipo mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku loyamba la mweziwo, muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena; likukhalireni inu tsiku lakuliza malipenga. Pamenepo muzipereka nsembe yopsereza ya fungo lokoma kwa Yehova; ng'ombe imodzi yamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi opanda chilema; ndi nsembe yao yaufa, ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a efa wa ng'ombeyo, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo, ndi limodzi la magawo khumi likhale la mwanawankhosa mmodzi, momwemo ndi anaankhosa asanu ndi awiri; ndi tonde mmodzi wa nsembe yauchimo, yakutetezera inu; pamodzi ndi nsembe yopsereza ya pamwezi, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, monga mwa lemba lake, zikhale za fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova. Ndipo tsiku la khumi la mwezi wachisanu ndi chiwiri uwu muzikhala nako kusonkhana kopatulika; pamenepo mudzichepetse, musamagwira ntchito; koma mubwere nayo nsembe yopsereza kwa Yehova, ya fungo lokoma; ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi; akhale kwa inu opanda chilema; ndi nsembe yao ya ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a efa wa ng'ombe, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo imodziyo; limodzi la magawo khumi likhale la mwanawankhosa mmodzi, momwemo ndi anaankhosa asanu ndi awiri; tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo, pamodzi ndi nsembe yauchimo yotetezera, ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira. Ndipo tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachisanu ndi chiwiri muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena, koma muchitire Yehova madyerero masiku asanu ndi awiri; ndipo mubwere nayo nsembe yopsereza, ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma kwa Yehova: ng'ombe zamphongo khumi ndi zitatu, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai, a chaka chimodzi, akhale opanda chilema; ndi nsembe yake yaufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a efa wa ng'ombe imodzi, momwemo nazo ng'ombe khumi ndi zitatuzo, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo imodzi, momwemo nazo nkhosa zamphongo ziwirizo; ndi limodzi la magawo khumi likhale la mwanawankhosa mmodzi, momwemo nao anaankhosa khumi ndi anai; ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira. Ndipo tsiku lachiwiri muzibwera nazo ng'ombe zamphongo khumi ndi ziwiri, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai a chaka chimodzi, opanda chilema; ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za anaankhosa, monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake; ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira. Ndi tsiku lachitatu ng'ombe khumi ndi imodzi, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai a chaka chimodzi opanda chilema; ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za anaankhosa monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake; ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira. Ndi tsiku lachinai ng'ombe khumi, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai, a chaka chimodzi, opanda chilema; nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za anaankhosa, monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake; ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira. Ndi tsiku lachisanu ng'ombe zisanu ndi zinai, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai, a chaka chimodzi, opanda chilema; ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za anaankhosa, monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake; ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira. Ndi tsiku lachisanu ndi chimodzi ng'ombe zisanu ndi zitatu, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai, a chaka chimodzi, opanda chilema; ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za anaankhosa, monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake; ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira. Ndi tsiku lachisanu ndi chiwiri ng'ombe zisanu ndi ziwiri, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai, a chaka chimodzi, opanda chilema; ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, za ng'ombe, za nkhosa yamphongo, ndi za anaankhosa, monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake; ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira. Tsiku lachisanu ndi chitatu muzikhala nalo tsiku loletsa; musamachita ntchito ya masiku ena; koma mubwere nayo nsembe yopsereza ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma kwa Yehova: ng'ombe imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, anaankhosa asanu ndi awiri, a chaka chimodzi, opanda chilema; nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za anaankhosa, monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake; ndi tonde mmodzi wa nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosakeleza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira. Izi muzikonzera Yehova mu zikondwerero zanu zoikika, pamodzi ndi zowinda zanu, ndi zopereka zanu zaufulu, za nsembe zanu zopsereza, ndi za nsembe zanu zaufa, ndi za nsembe zanu zothira, ndi za nsembe zanu zoyamika. Ndipo Mose ananena ndi ana a Israele monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose. Ndipo Mose ananena ndi akulu a mafuko a ana a Israele, nati, Chinthu anachilamulira Yehova ndi ichi: Munthu akachitira Yehova chowinda, kapena akalumbira lumbiro ndi kumangira moyo wake chodziletsa, asaipse mau ake; azichita monga mwa zonse zotuluka m'kamwa mwake. Ndipo mkazi akachitira Yehova chowinda, nakadzimanga nacho chodziletsa, pokhala ali m'nyumba ya atate wake, m'unamwali; ndipo atate wake akamva chowinda chake, ndi chodziletsa chake anamanga moyo wake nacho, koma wakhala naye chete atate wake; pamenepo zowinda zake zonse zidzakhazikika, ndi chodziletsa chilichonse wamanga nacho moyo wake chidzakhazikika. Koma atate wake akamletsa tsiku lakumva iye; zowinda zake zonse, ndi zodziletsa zake zonse anamanga nazo moyo wake, sizidzakhazikika; ndipo Yehova adzamkhululukira, popeza atate wake anamletsa. Ndipo akakwatibwa naye mwamuna, pokhala ali nazo zowinda zake, kapena zonena zopanda pake za milomo yake, zimene anamanga nazo moyo wake; nakazimva mwamuna wake, nakakhala naye chete tsiku lakuzimva iye; pamenepo zowinda zake zidzakhazikika, ndi zodziletsa anamanga nazo moyo wake zidzakhazikika. Koma mwamuna wake akamletsa tsiku lakumva iye; pamenepo adzafafaniza chowinda chake anali nacho, ndi zonena zopanda pake za milomo yake, zimene anamanga nazo moyo wake; ndipo Yehova adzamkhululukira. Koma chowinda cha mkazi wamasiye, kapena mkazi wochotsedwa, zilizonse anamanga nazo moyo wake zidzamkhazikikira. Ndipo ngati anawinda m'nyumba ya mwamuna wake, kapena anamanga moyo wake ndi chodziletsa ndi kulumbirapo, ndipo mwamuna wake anamva, koma anakhala naye chete osamletsa, pamenepo zowinda zake zonse zidzakhazikika, ndi zodziletsa zonse anamanga nazo moyo wake zidzakhazikika. Koma ngati mwamuna wake anazifafanizadi tsiku lakuzimva iye, zonse zotuluka m'milomo yake kunena za zowinda zake, kapena za chodziletsa cha moyo wake sizidzakhazikika; ndipo Yehova adzamkhululukira iye. Chowinda chilichonse, ndi cholumbira chilichonse chodziletsa chakuchepetsa nacho moyo, mwamuna wake achikhazikira, kapena mwamuna wake achifafaniza. Koma mwamuna wake akhala naye chete tsiku ndi tsiku; pamenepo akhazikira zowinda zake zonse, kapena zodziletsa zake zonse, zili pa iye; wazikhazikitsa, popeza anakhala naye chete tsikuli anazimva iye. Koma akazifafaniza atatha kuzimva; pamenepo adzasenza mphulupulu yake. Awa ndi malemba amene Yehova analamulira Mose, a pakati pa mwamuna ndi mkazi wake, pakati pa atate ndi mwana wake wamkazi, akali namwali, m'nyumba ya atate wake. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Abwezereni chilango Amidiyani chifukwa cha ana a Israele; utatero udzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wako. Ndipo Mose ananena ndi anthu, nati, Adzikonzere ena mwa inu zida za nkhondo, alimbane nao Amidiyani, kuwabwezera Amidiyani chilango cha Yehova. Muwatume kunkhondo a fuko limodzi, chikwi chimodzi, atere mafuko onse a Israele. Ndipo anapereka mwa zikwi za Israele, a fuko limodzi chikwi chimodzi, anthu zikwi khumi ndi ziwiri okonzekeratu ndi zankhondo. Ndipo Mose anawatuma a fuko limodzi chikwi chimodzi, kunkhondo, iwowa ndi Finehasi mwana wa Eleazara wansembe, kunkhondo, ndi zipangizo zopatulika, ndi malipenga oliza m'dzanja lake. Ndipo anawathira nkhondo Amidiyani, monga Yehova adamuuza Mose; nawapha amuna onse. Ndipo anapha mafumu a Amidiyani pamodzi ndi ophedwa ao ena; ndiwo Evi, ndi Rekemu, ndi Zuri, ndi Huri, ndi Reba, mafumu asanu a Amidiyani; namupha Balamu mwana wa Beori ndi lupanga. Ndipo ana a Israele anagwira akazi a Amidiyani, ndi ana ang'ono, nafunkha ng'ombe zao zonse, ndi zoweta zao zonse, ndi chuma chao chonse. Ndipo anatentha ndi moto midzi yao yonse yokhalamo iwo, ndi zigono zao zonse. Ndipo anapita nazo zofunkha zonse, ndi zakunkhondo zonse, ndizo anthu ndi nyama. Ndipo anadza nao andende, ndi zakunkhondo, ndi zofunkha, kwa Mose, ndi kwa Eleazara wansembe, ndi kwa khamu la ana a Israele, kuchigono, ku zidikha za Mowabu, zili ku Yordani pafupi pa Yeriko. Ndipo Mose, ndi Eleazara wansembe, ndi akalonga onse a khamulo, anatuluka kukomana nao kunja kwa chigono. Ndipo Mose anakwiya nao akazembe a nkhondoyi, atsogoleri a zikwi, atsogoleri a mazana, akufuma kunkhondo adaithira. Ndipo Mose ananena nao, Kodi mwasunga ndi moyo akazi onse? Taonani, awa analakwitsa ana a Israele pa Yehova ndi cha Peori chija, monga adawapangira Balamu; kotero kuti kunali mliri m'khamu la Yehova. Ndipo tsono iphani amuna onse mwa anawo, iphaninso akazi onse akudziwa mwamuna mogona naye. Koma ana akazi onse osadziwa mwamuna mogona naye, asungeni ndi moyo akhale anu. Ndipo mukhale m'misasa kunja kwa chigono masiku asanu ndi awiri; aliyense adapha munthu, ndi aliyense wakukhudza wophedwa, mudziyeretse tsiku lachitatu ndi lachisanu ndi chiwiri, inu ndi andende anu. Muyeretse zovala zanu zonse, zipangizo zonse zachikopa, ndi zoomba zonse za ubweya wa mbuzi, ndi zipangizo zonse za mtengo. Ndipo Eleazara wansembe ananena ndi ankhondo adapita kunkhondowo, Lemba la chilamulocho Yehova analamulira Mose ndi ili: Golide, ndi siliva, mkuwa, chitsulo, ndolo ndi mtovu zokha, zonse zakulola moto, mupititse m'moto, ndipo zidzakhala zoyera; koma muziyeretsenso ndi madzi akusiyanitsa. Koma zonse zosalola moto, muzipititse m'madzi. Ndipo muzitsuke zovala zanu tsiku lachisanu ndi chiwiri, kuti mukhale oyera; ndipo mutatero mulowe m'chigono. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Werengani zakunkhondo, ndizo anthu, ndi zoweta, iwe, ndi Eleazara wansembe, ndi akulu a nyumba za makolo za khamulo; nugawe zakunkhondo pawiri; pakati pa othira nkhondo amene anatuluka kunkhondo, ndi khamu lonse. Ndipo usonkhetse anthu ankhondo akutuluka kunkhondo apereke kwa Yehova: munthu mmodzi mwa anthu mazana asanu, mwa ng'ombe, mwa abulu, mwa nkhosa ndi mbuzi, momwemo. Uzitenge ku gawo lao, ndi kuzipereka kwa Eleazara wansembe, zikhale nsembe yokweza ya Yehova. Ndipo ku gawo la ana a Israele utenge munthu mmodzi mwa anthu makumi asanu, mwa ng'ombe, mwa abulu, mwa nkhosa ndi mbuzi, mwa zoweta zonse, momwemo; nuzipereke kwa Alevi, akusunga udikiro wa Kachisi wa Yehova. Ndipo Mose ndi Eleazara wansembe anachita monga Yehova anamuuza Mose. Ndipo zakunkhondo, zotsalira zofunkha zonse adazifunkha ankhondowa, ndizo nkhosa zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu zikwi makumi asanu ndi awiri kudza zisanu, ndi ng'ombe zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu ziwiri, ndi abulu zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu chimodzi, ndi anthu, ndiwo akazi osadziwa mwamuna mogona naye, onse pamodzi zikwi makumi atatu ndi ziwiri. Ndipo limodzi la magawo awiri, ndilo gawo la iwo adatuluka kunkhondo, linafikira nkhosa zikwi mazana atatu mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu. Ndi msonkho wa Yehova wankhosa ndiwo mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu. Ndipo ng'ombe zidafikira zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi chimodzi; pamenepo msonkho wa Yehova ndiwo makumi asanu ndi awiri mphambu ziwiri. Ndipo abulu anafikira zikwi makumi atatu ndi mazana asanu; pamenepo msonkho wa Yehova ndiwo makumi asanu ndi limodzi mphambu mmodzi. Ndipo anthu anafikira zikwi khumi ndi zisanu ndi chimodzi; pamenepo msonkho wa Yehova ndiwo anthu makumi atatu mphambu awiri. Ndipo Mose anapereka zamsonkhozo, ndizo nsembe yokweza ya Yehova, kwa Eleazara wansembe, monga Yehova adamuuza Mose. Ndipo kunena za gawo la ana a Israele, limene Mose adalichotsa kwa anthu ochita nkhondowo, (ndipo gawo la khamulo ndilo nkhosa zikwi mazana atatu mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu, ndi ng'ombe zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi chimodzi, ndi abulu zikwi makumi atatu ndi mazana asanu, ndi anthu zikwi khumi ndi zisanu ndi chimodzi,) mwa gawolo la ana a Israele Mose anatenga munthu mmodzi mwa makumi asanu, ndi zoweta momwemo, nazipereka kwa Alevi, akusunga udikiro wa Kachisi wa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose. Pamenepo akazembe a pa ankhondo zikwi, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, anayandikiza kwa Mose; nati kwa Mose, Atumiki anu anawerenga ankhondo tinali nao, ndipo sanasowe munthu mmodzi wa ife. Ndipo tabwera nacho chopereka cha Yehova, yense chimene anachipeza, zokometsera zagolide, unyolo, zikwinjiri, mphete zosindikizira, nsapule, ndi mkanda, kuchita chotetezera moyo wathu pamaso pa Yehova. Ndipo Mose ndi Eleazara wansembe analandira golideyo kwa iwowo, ndizo zokometsera zonse zokonzeka. Ndipo golide yense wa nsembe yokweza ya Yehova amene anapereka kwa Yehova, wofuma kwa atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndiwo masekeli zikwi khumi ndi zisanu ndi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu. Popeza wankhondo yense anadzifunkhira yekha. Ndipo Mose ndi Eleazara wansembe analandira golide kwa akulu a zikwi ndi a mazana, nalowa naye ku chihema chokomanako, chikumbutso cha ana a Israele pamaso pa Yehova. Koma ana a Rubeni ndi ana Gadi anali nazo zoweta zambirimbiri; ndipo anapenyerera dziko la Yazere, ndi dziko la Giliyadi, ndipo taonani, malowo ndiwo malo a zoweta. Pamenepo ana a Gadi ndi ana a Rubeni anadza nanena ndi Mose, ndi Eleazara wansembe, ndi akalonga a khamulo, nati, Ataroti, ndi Diboni, ndi Yazere, ndi Nimira, ndi Hesiboni, ndi Eleyale, ndi Sibima, ndi Nebo, ndi Beoni, dzikoli Yehova analikantha pamaso pa khamu la Israele, ndilo dziko la zoweta ndipo anyamata anu ali nazo zoweta. Ndipo anati, Ngati tapeza ufulu pamaso panu, mupatse anyamata anu dziko ili likhale laolao; tisaoloke Yordani. Ndipo Mose anati kwa ana a Gadi ndi ana a Rubeni, Kodi abale anu apite kunkhondo, ndi inu mukhale pansi kuno? Ndipo mufoketseranji mtima wa ana a Israele kuti asaoloke ndi kulowa dzikoli Yehova anawapatsa? Anatero makolo anu, muja ndinawatumiza achoke ku Kadesi-Baranea kukaona dziko. Popeza atakwera kunka ku chigwa cha Esikolo, naona dziko, anafoketsa mtima wa ana a Israele, kuti asalowe dzikoli Yehova adawapatsa. Ndipo Yehova anapsa mtima tsiku lija, nalumbira Iye, nati, Anthu adakwerawo kutuluka m'Ejipito, kuyambira wa zaka makumi awiri ndi mphambu sadzaona dziko limene ndinalumbirira Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo; popeza sananditsate Ine ndi mtima wonse; koma Kalebe mwana wa Yefune, Mkenizi, ndi Yoswa mwana wa Nuni ndiwo; popeza anatsata Yehova ndi mtima wonse. Ndipo Yehova anapsa mtima pa Israele, nawayendetsayendetsa m'chipululu zaka makumi anai, kufikira utatha mbadwo wonsewo udachita choipa pamaso pa Yehova. Ndipo taonani, mwauka m'malo mwa makolo anu, gulu la anthu ochimwa, kuonjezanso mkwiyo waukali wa Yehova pa Israele. Pakuti mukabwerera m'mbuyo kusamtsata Iye, adzawasiyanso m'chipululu, ndipo mudzaononga anthu awa onse. Ndipo anayandikiza, nati Tidzamangira zoweta zathu makola kuno, ndi ana athu midzi; koma ife tidzakhala okonzeka ndi kufulumira pamaso pa ana a Israele, kufikira tidawafikitsa kumalo kwao; ndi ang'ono athu adzakhala m'midzi ya malinga chifukwa cha okhala m'dzikomo. Sitidzabwerera kwathu, kufikira ana a Israele atalandira yense cholowa chake. Pakuti sitidzalandira pamodzi nao tsidya la Yordani, ndi m'tsogolo mwake; popeza cholowa chathu tachilandira tsidya lino la Yordani kum'mawa. Ndipo Mose anati nao, Ngati mudzachita ichi, ndi kudzikonza kunkhondo pamaso pa Yehova, ndi kuoloka Yordani pamaso pa Yehova okonzeka onse mwa inu, kufikira atapirikitsa adani ake pamaso pake, ndi dziko lagonjera Yehova; mutatero mudzabwerere, ndi kukhala osachimwira Yehova ndi Israele; ndipo dziko ili lidzakhala lanulanu pamaso pa Yehova. Koma mukapanda kutero, taonani, mwachimwira Yehova; ndipo zindikirani kuti tchimo lanu lidzakupezani. Dzimangireni midzi ya ana anu, ndi makola a zoweta zanu; ndipo muzichite zotuluka m'kamwa mwanu. Ndipo ana a Gadi ndi ana a Rubeni ananena ndi Mose, nati, Anyamata anu adzachita monga mbuyanga alamulira. Ana athu, akazi athu, zoweta zathu, ndi ng'ombe zathu zonse, zidzakhala komweko m'midzi ya ku Giliyadi; koma anyamata anu adzaoloka, yense wokonzekera ndi zankhondo pamaso pa Yehova kunkhondo, monga wanena mbuyanga. Pamenepo Mose anamuuza Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a makolo a mafuko a ana a Israele za iwo. Ndipo Mose anati kwa iwo, Ngati ana a Gadi ndi ana a Rubeni aoloka nanu Yordani, yense wokonzekera ndi zankhondo pamaso pa Yehova, ndi dziko lagonjera inu; pamenepo muwapatse dziko la Giliyadi likhale laolao; koma akapanda kuoloka nanu okonzeka, akhale nao maiko aoao pakati pa inu m'dziko la Kanani. Ndipo ana a Gadi ndi ana a Rubeni anayankha, nati, Monga Yehova anati kwa anyamata anu momwemo tidzachita. Tidzaoloka okonzeka pamaso pa Yehova ku dziko la Kanani, koma cholowa chathuchathu chikhale tsidya lino la Yordani. Ndipo Mose anawapatsa, ndiwo ana a Gadi, ndi ana a Rubeni ndi fuko la hafu la Manase mwana wa Yosefe, dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani, dzikoli ndi midzi yake m'malire mwao, ndiyo midzi ya dziko lozungulirako. Ndipo ana a Gadi anamanga Diboni, ndi Ataroti, ndi Aroere; Ataroti-Sofani, Yazere, ndi Yogobeha; ndi Betenimura, ndi Beteharani: midzi ya m'malinga, ndi makola a zoweta. Ndipo ana a Rubeni anamanga Hesiboni, ndi Eleyale, ndi Kiriyataimu; ndi Nebo, ndi Baala-Meoni (anasintha maina ao), ndi Sibima; ndipo anaitcha midzi adaimanga ndi maina ena. Ndipo ana a Makiri mwana wa Manase ananka ku Giliyadi, naulanda, napirikitsa Aamori anali m'mwemo. Ndipo Mose anapatsa Makiri mwana wa Manase Giliyadi; ndipo anakhala m'menemo. Ndipo Yairi mwana wa Manase ananka nalanda midzi yao, naitcha Havoti-Yairi. Ndipo Noba ananka nalanda Kenati, ndi milaga yake, nautcha Noba, dzina lake. Maulendo a ana a Israele amene anatuluka m'dziko la Ejipito monga mwa makamu ao, ndi dzanja la Mose ndi Aroni, ndi awa. Ndipo Mose analembera matulukidwe ao monga mwa maulendo ao, monga mwa mau a Yehova; ndipo maulendo ao ndi awa monga mwa matulukidwe ao. Ndipo anachokera ku Ramsesi mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi woyamba; atachita Paska m'mawa mwake ana a Israele, anatuluka ndi dzanja lokwezeka pamaso pa Aejipito onse, pamene Aejipito analikuika oyamba kubadwa ao onse, amene Yehova adawakantha; Yehova adaweruzanso milungu yao. Ndipo ana a Israele anachokera ku Ramsesi, nayenda namanga ku Sukoti. Nachokera ku Sukoti, nayenda namanga m'Etamu, ndiko ku malekezero a chipululu. Ndipo anachokera ku Etamu, nayenda nabwerera ku Pihahiroti, ndiko kutsogolo kwake kwa Baala-Zefoni; namanga iwo patsogolo pa Migidoli. Ndipo anachokera ku Pihahiroti, naoloka pakati pa nyanja nalowa m'chipululu; nayenda ulendo wa masiku atatu m'chipululu cha Etamu, namanga m'Mara. Ndipo anachokera ku Mara, nayenda nafika ku Elimu, ku Elimu ndiko kuli akasupe khumi ndi awiri a madzi, ndi akanjedza makumi asanu ndi awiri; namanga iwo komweko. Ndipo anachokera ku Elimu, nayenda namanga ku Nyanja Yofiira. Nachokera ku Nyanja Yofiira, nayenda namanga m'chipululu cha Sini. Nachokera ku chipululu cha Sini, nayenda namanga m'Dofika. Nachokera ku Dofika, nayenda namanga m'Alusi. Nachokera ku Alusi, nayenda namanga m'Refidimu; kumeneko kunalibe madzi kuti anthu amwe. Ndipo anachokera ku Refidimu, nayenda namanga m'chipululu cha Sinai. Nachokera ku chipululu cha Sinai, nayenda namanga m'Kibroti-Hatava. Nachokera ku Kibroti-Hatava, nayenda namanga m'Hazeroti. Nachokera ku Hazeroti, nayenda namanga m'Ritima. Nachokera ku Ritima, nayenda namanga m'Rimoni-Perezi. Nachokera ku Rimoni-Perezi, nayenda namanga m'Libina. Nachokera ku Libina, nayenda namanga m'Risa. Nachokera Risa, nayenda namanga m'Kehelata. Nachokera ku Kehelata, nayenda namanga m'phiri la Sefera. Nachokera kuphiri la Sefera, nayenda namanga m'Harada. Nachokera ku Harada, nayenda namanga m'Makeloti. Nachokera ku Makeloti, nayenda namanga m'Tahata. Nachokera ku Tahata, nayenda namanga m'Tera. Nachokera ku Tera, nayenda namanga m'Mitika. Nachokera ku Mitika, nayenda namanga m'Hasimona. Nachokera ku Hasimona, nayenda namanga m'Meseroti. Nachokera ku Meseroti, nayenda namanga m'Bene-Yaakani. Nachokera ku Bene-Yaakani, nayenda namanga m'Hori Hagidigadi. Nachokera ku Hori Hagidigadi, nayenda namanga m'Yotibata. Nachokera ku Yotibata, nayenda namanga m'Aborona. Nachokera ku Aborona, nayenda namanga m'Eziyoni-Gebere. Nachokera ku Eziyoni-Gebere, nayenda namanga m'chipululu cha Zini (ndiko Kadesi). Nachokera ku Kadesi, nayenda namanga m'phiri la Hori, ku malekezero a dziko la Edomu. Ndipo Aroni wansembe anakwera m'phiri la Hori pa mau a Yehova, nafa komweko, atatuluka ana a Israele m'dziko la Ejipito zaka makumi anai, mwezi wachisanu, tsiku loyamba la mwezi. Ndipo Aroni ndiye wa zaka zana limodzi mphambu makumi awiri kudza zitatu pakufa iye m'phiri la Hori. Ndipo Mkanani, mfumu ya Aradi, wakukhala kumwera m'dziko la Kanani, anamva za kudza kwao kwa ana a Israele. Ndipo anachokera kuphiri la Hori, nayenda namanga m'Zalimona. Nachokera ku Zalimona, nayenda namanga m'Punoni. Nachokera ku Punoni, nayenda namanga m'Oboti. Nachokera ku Oboti, nayenda namanga m'Iyeabarimu, m'malire a Mowabu. Nachokera ku Iyimu, nayenda namanga m'Diboni Gadi. Nachokera ku Diboni Gadi, nayenda namanga m'Alimoni-Dibulataimu. Nachokera ku Alimoni-Dibulataimu, nayenda namanga m'mapiri a Abarimu, chakuno cha Nebo. Nachokera ku mapiri a Abarimu, nayenda namanga m'zidikha za Mowabu pa Yordani ku Yeriko. Ndipo anamanga pa Yordani, kuyambira ku Beteyesimoti kufikira ku Abele-Sitimu m'zidikha za Mowabu. Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'zidikha za Mowabu pa Yordani ku Yeriko, nati, Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mutaoloka Yordani kulowa m'dziko la Kanani, mupirikitse onse okhala m'dziko pamaso panu, ndi kuononga mafano ao onse a miyala, ndi kuononga mafano ao onse oyenga, ndi kupasula misanje yao yonse; ndipo mulande dziko, ndi kukhala m'mwemo, pakuti ndinakupatsani inu dzikoli likhale lanulanu. Ndipo mulandire dzikoli ndi kuchita maere monga mwa mabanja anu; cholowa chao chichulukire ochulukawo, cholowa chao chichepere ochepawo; kumene maere amgwera munthu, kumeneko nkwake; mulandire cholowa chanu monga mwa mafuko a makolo anu. Koma mukapanda kupirikitsa okhala m'dziko pamaso panu, pamenepo iwo amene muwalola atsale adzakhala ngati zotwikira m'maso mwanu, ndi minga m'mbali zanu, nadzakuvutani m'dziko limene mukhalamo. Ndipo kudzakhala kuti monga ndinayesa kuchitira iwowa, ndidzakuchitirani inu. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Uza ana a Israele, nunene nao, Mutalowa m'dziko la Kanani, ndilo dziko logwera inu, likhale cholowa chanu, dziko la Kanani monga mwa malire ake, dera lanu la kumwera lidzakhala lochokera ku chipululu cha Zini, kutsata m'mphepete mwa Edomu, ndi malire anu a kumwera adzakhala ochokera ku malekezero a Nyanja ya Mchere kum'mawa; ndi malire anu adzapinda kuchokera kumwera kunka pokwera Akarabimu, ndi kupitirira ku Zini; ndi kutuluka kwake adzachokera kumwera ku Kadesi-Baranea, nadzatuluka kunka ku Hazara-Adara, ndi kupita kunka ku Azimoni; ndipo malirewo adzapinda ku Azimoni kunka ku mtsinje wa Ejipito, ndi kutuluka kwao adzatuluka kunyanja. Kunena za malire a kumadzulo Nyanja Yaikulu ndiyo malire anu; ndiyo malire anu a kumadzulo. Malire anu a kumpoto ndiwo: kuyambira ku Nyanja Yaikulu mulinge kuphiri la Hori: kuchokera kuphiri la Hori mulinge polowera Hamati; ndipo kutuluka kwake kwa malire kudzakhala ku Zedadi. Ndipo malirewo adzatuluka kunka ku Zifuroni, ndi kutuluka kwake kudzakhala ku Hazara-Enani; ndiwo malire anu a kumpoto. Ndipo mudzilembere malire a kum'mawa ochokera ku Hazara-Enani kunka ku Sefamu; ndi malire adzatsika ku Sefamu kunka ku Ribula, kum'mawa kwa Aini; ndipo malire adzatsika, nadzafikira mbali ya nyanja ya Kinereti kum'mawa, ndi malire adzatsika ku Yordani, ndi kutuluka kwake kudzakhala ku Nyanja ya Mchere; ili ndili dziko lanu monga mwa malire ake polizinga. Ndipo Mose anauza ana a Israele, nati, Ili ndi dzikoli mudzalandira ndi kuchita maere, limene Yehova analamulira awapatse mafuko asanu ndi anai ndi hafu; popeza fuko la ana a Rubeni monga mwa nyumba za makolo ao, ndi fuko la ana a Gadi monga mwa nyumba za makolo ao, adalandira, ndi fuko la hafu la Manase lalandira cholowa chao; mafuko awiriwa ndi hafu adalandira cholowa chao tsidya lija la Yordani ku Yeriko, kum'mawa, kotulukira dzuwa. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Maina a amunawo adzakugawirani dziko likhale cholowa chanu, ndi awa: Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni. Muwatengenso akalonga, kalonga mmodzi ku fuko limodzi, agawe dziko likhale cholowa chao. Maina a amunawo ndiwo: wa fuko la Yuda, Kalebe mwana wa Yefune. Wa fuko la ana a Simeoni, Semuele mwana wa Amihudi. Wa fuko la Benjamini, Elidadi mwana wa Kisiloni. Wa fuko la ana a Dani, kalonga Buki mwana wa Yogili. Wa ana a Yosefe; wa fuko la ana a Manase, kalonga Haniyele mwana wa Efodi. Wa fuko la ana a Efuremu, kalonga Kemuwele mwana wa Sifutani. Wa fuko la ana a Zebuloni, kalonga Elizafani mwana wa Paranaki. Wa fuko la ana a Isakara, kalonga Palatiele mwana wa Azani. Wa fuko la ana a Asere, kalonga Ahihudi mwana wa Selomi. Wa fuko la ana a Nafutali, kalonga Pedahele mwana wa Amihudi. Iwo ndiwo amene Yehova analamulira agawire ana a Israele cholowa chao m'dziko la Kanani. Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'zidikha za Mowabu, pa Yordani, ku Yeriko, ndi kuti, Uza ana a Israele, kuti apatseko Alevi cholowa chaochao, midzi yokhalamo; muwapatsenso Alevi mabusa akuzungulira midzi. Ndipo midzi ndiyo yokhalamo iwowa; ndi mabusa akhale a ng'ombe zao, ndi zoweta zao, inde nyama zao zonse. Ndipo mabusa a midziyo, imene muipereke kwa Alevi ndiwo a mikono chikwi chimodzi kuyambira kulinga kufikira kunja. Ndipo muyese kunja kwa mudzi, mbali ya kum'mawa mikono zikwi ziwiri, ndi mbali ya kumwera mikono zikwi ziwiri, ndi mbali ya kumadzulo mikono zikwi ziwiri, ndi mbali ya kumpoto mikono zikwi ziwiri; ndi mudziwo pakati; ndiwo mabusa a kumidzi. Ndipo midziyo muipereke kwa Alevi ndiyo midzi ija isanu ndi umodzi yopulumukirako; imene muipereke kuti wakupha mnzake athawireko; ndipo pamodzi ndi iyi muperekenso midzi makumi anai ndi iwiri. Midzi yonse muipereke kwa Alevi ndiyo midzi makumi anai ndi isanu ndi itatu, iyo pamodzi ndi mabusa ao. Ndipo kunena za midziyo muiperekeyo yaoyao ya ana a Israele, okhala nayo yambiri mutengeko yambiri; okhala nayo pang'ono mutengeko pang'ono; onse operekako midzi yao kwa Alevi monga mwa cholowa chao adachilandira. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Pakuoloka inu Yordani kulowa m'dziko la Kanani, muikire midzi ikukhalireni midzi yopulumukirako; kuti wakupha mnzake wosati dala athawireko. Ndipo midziyo ikukhalireni yakupulumuka wolipsa; kuti wakupha mnzake asafe, kufikira ataima pamaso pa msonkhano amweruze. Ndipo midziyo muipereke ikukhalireni midzi isanu ndi umodzi yopulumukirako. Mupereke midzi itatu tsidya lino la Yordani, ndi midzi itatu mupereke m'dziko la Kanani, ndiyo yopulumukirako. Midzi isanu ndi umodzi imene ndiyo yopulumukirako ana a Israele, ndi mlendo, ndi wokhala pakati pao; kuti aliyense adamupha munthu osati dala athawireko. Koma akamkantha ndi chipangizo chachitsulo, kuti wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu. Kapena akamkantha m'dzanja muli mwala, wakufetsa munthu, ndipo wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu. Kapena akamkantha m'dzanja muli chipangizo chamtengo, chakufetsa munthu, ndipo wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu. Wolipsa mwazi mwini wake aphe wakupha munthuyo; pakumpeza amuphe. Ndipo akampyoza momkwiyira, kapena kumponyera kanthu momlalira, kuti wafa; kapena kumpanda ndi dzanja lake momuda, kuti wafa, womkanthayo nayenso amuphe ndithu; ndiye wakupha munthu; wolipsa mwazi aphe wakupha munthuyo akampeza. Koma akampyoza modzidzimuka, osamuda, kapena kumponyera kanthu osamlalira, kapena kumponyera mwala wakufetsa munthu, osamuona, namgwetsera uwu, kuti wafa, koma sindiye mdani wake, kapena womfunira choipa; pamenepo msonkhano uziweruza pakati pa wokantha mnzakeyo ndi wolipsa mwaziyo monga mwa maweruzo awa; ndipo msonkhano umlanditse wakupha munthu m'dzanja la wolipsa mwazi, ndi msonkhanowo umbwezere kumudzi wake wopulumukirako, kumene adathawirako; ndipo azikhalamo kufikira atafa mkulu wa ansembe wodzozedwa ndi mafuta opatulika. Koma wakupha munthu akatuluka nthawi iliyonse kulumpha malire a mudzi wake wopulumukirako kumene anathawirako; nakampeza wolipsa mwazi kunja kwa malire a mudzi wake wothawirako, ndipo wolipsa mwazi akapha wakupha munthu, alibe kuchimwira mwazi; popeza wakupha munthu akadakhala m'mudzi wake wopulumukirako kufikira atafa mkulu wa ansembe; koma atafa mkulu wa ansembe wakupha munthuyo abwere ku dziko lakelake. Ndipo izi zikhale kwa inu lemba la chiweruzo mwa mibadwo yanu, m'nyumba zanu zonse. Aliyense wakantha munthu, wakupha munthuyo aziphedwa pakamwa pa mboni; koma mboni ya munthu mmodzi isafikire kuti munthu afe. Musamalandira dipo lakuombola moyo wa iye adapha munthu, napalamula imfa; koma aziphedwa ndithu. Musamalandira dipo lakuombola iye amene adathawira kumudzi wake wopulumukirako, kuti abwerenso kukhala m'dziko, kufikira atafa mkulu wa ansembe. Ndipo musamaipsa dziko muli m'mwemo; popeza mwazi uipsa dziko; pakuti kulibe kutetezera dziko chifukwa cha mwazi anaukhetsa m'mwemo, koma ndi mwazi wa iye anaukhetsa ndiwo. Usamadetsa dziko ukhala m'mwemo, limene ndikhalitsa pakati pake; popeza Ine Yehova ndikhalitsa pakati pa ana a Israele. Ndipo akulu a makolo a mabanja a ana a Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase, wa mabanja a ana a Yosefe, anayandikiza, nanena pamaso pa Mose, ndi pamaso pa akalonga, ndiwo akulu a makolo a ana a Israele; nati, Yehova analamulira mbuye wanga mupatse ana a Israele dzikoli mochita maere likhale cholowa chao; ndipo Yehova analamulira mbuye wathu mupatse ana ake akazi cholowa cha Zelofehadi mbale wathu. Ndipo akakwatibwa nao ana amuna a mafuko ena a ana a Israele, achichotse cholowa chao ku cholowa cha makolo athu, nachionjeze ku cholowa cha fuko limene adzakhalako; chotero achichotse ku maere a cholowa chathu. Ndipo pofika chaka choliza cha ana a Israele adzaphatikiza cholowa chao ku cholowa cha fuko limene akhalako; chotero adzachotsa cholowa chao ku cholowa cha fuko la makolo athu. Ndipo Mose analamulira ana a Israele monga mwa mau a Yehova, nati, Fuko la ana a Yosefe linena zoona. Cholamulira Yehova za ana akazi a Zelofehadi ndi ichi, kuti, Akwatibwe nao amene afuna eni ake; komatu akwatibwe nao a banja la fuko la makolo ao okhaokha. Motero cholowa cha ana a Israele sichidzanka ku fuko ndi fuko; popeza ana a Israele adzamamatira yense ku cholowa cha fuko la makolo ake. Ndipo mwana wamkazi yense wa mafuko a ana a Israele, wakukhala nacho cholowa, akwatibwe ndi wina wa banja la fuko la kholo lake, kuti ana a Israele akhale nacho yense cholowa cha makolo ake. Motero cholowa cha ana a Israele sichidzanka ku fuko ndi fuko, pakuti mafuko a ana a Israele adzamamatira lonse ku cholowa chakechake. Monga Yehova adalamulira Mose, momwemo ana akazi a Zelofehadi anachita; popeza Mala, Tiriza, ndi Hogila, ndi Milika, ndi Nowa, ana akazi a Zelofehadi, anakwatibwa ndi ana amuna a abale a atate wao. Anakwatibwa mwa mabanja a ana a Manase mwana wa Yosefe; ndipo cholowa chao chinakhala m'fuko la banja la atate wao. Awa ndi malamulo ndi maweruzo, amene Yehova analamulira ana a Israele ndi dzanja la Mose m'zidikha za Mowabu pa Yordani ku Yeriko. Awa ndi mau amene Mose ananena kwa Israele wonse, tsidya la Yordani m'chipululu, m'chidikha cha pandunji pa Sufu, pakati pa Parani, ndi Tofele, ndi Labani, ndi Hazeroti, ndi Dizahabu. Ulendo wake wochokera ku Horebu wofikira ku Kadesi-Baranea, wodzera njira ya phiri la Seiri, ndiwo wa masiku khumi ndi limodzi. Ndipo kunali, chaka cha makumi anai, mwezi wakhumi ndi umodzi, tsiku loyamba la mweziwo, Mose ananena ndi ana a Israele, monga mwa zonse Yehova adamlamulira awauze; atakantha Sihoni mfumu ya Aamori, wakukhala m'Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya Basani, wakukhala m'Asitaroti, ku Ederei. Tsidya lija la Yordani, m'dziko la Mowabu, Mose anayamba kufotokozera chilamulo ichi, ndi kuti, Yehova Mulungu wathu ananena ndi ife m'Horebu, ndi kuti Yakwanira nthawi yokhala inu m'phiri muno; bwererani, yendani ulendo wanu ndi kumuka ku mapiri a Aamori, ndi koyandikizana nao, kuchidikha, kumapiri, ndi kunsi ndi kumwera, ndi kumphepete kwa nyanja, dziko la Akanani, ndi Lebanoni, kufikira mtsinje waukulu wa Yufurate. Taonani, ndakupatsani dzikoli pamaso panu, lowani landirani dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, kuti ili ndidzawapatsa iwo ndi mbeu zao pambuyo pao. Ndipo muja ndinanena ndi inu, ndi kuti, Sinditha ine kukunyamulani ndekha; Yehova Mulungu wanu anakuchulukitsani, ndipo taonani, lero muchuluka ngati nyenyezi za kumwamba. Yehova Mulungu wa makolo anu, achulukitsire chiwerengero chanu chalero ndi chikwi chimodzi, nakudalitseni monga Iye ananena nanu! Ndikasenza bwanji ndekha kupsinya kwanu, ndi katundu wanu, ndi kulimbana kwanu? Dzifunireni amuna anzeru, ndi ozindikira bwino, ndi odziwika mwa mafuko anu, ndipo ndidzawaika akhale akulu anu. Pamenepo munandiyankha ndi kuti, Mau mwanenawa ndi abwino kuwachita. Potero ndinatenga akulu a mafuko anu, amuna anzeru, ndi odziwika, ndi kuwaika akhale akulu anu, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndi atsogoleri a makumi, ndi akapitao, a mafuko anu. Ndipo ndinauza oweruza anu muja, ndi kuti, Mverani milandu ya pakati pa abale anu, ndi kuweruza kolungama pakati pa munthu ndi mbale wake, ndi mlendo wokhala naye. Musamasamalira munthu poweruza mlandu; ang'ono ndi akulu muwamvere chimodzimodzi; musamaopa nkhope ya munthu; popeza chiweruzo ncha Mulungu; ndipo mlandu ukakukanikani mubwere nao kwa ine, ndidzaumva. Ndipo ndinakuuzani muja zonse muyenera kuzichita. Pamenepo tinayenda ulendo kuchokera ku Horebu, ndi kubzola m'chipululu chachikulu ndi choopsa chija chonse munachionachi, pa njira ya ku mapiri a Aamori, monga Yehova Mulungu wathu anatiuza; ndipo tinadza ku Kadesi-Baranea. Ndipo ndinati kwa inu, Mwafikira mapiri a Aamori, amene Yehova Mulungu wathu atipatsa. Taonani, Yehova Mulungu wanu wapatsa dzikoli pamaso panu; kwerakoni, landirani, monga Yehova Mulungu wa makolo anu, wanena ndi inu; musamachita mantha, musamatenga nkhawa. Ndipo munayandikiza kwa ine inu nonse, ndi kuti, Titumize amuna atitsogolere, kuti akatizondere dziko ndi kutibwezera mau akunena za njira ya kukwera nayo ife pomka komwemo, ndi za midzi yoti tidzafikako. Ndipo chinandikomera chinthu ichi; ndipo ndinatenga amuna khumi ndi awiri a inu, fuko limodzi mwamuna mmodzi; amenewa anatembenuka nakwera kumapiri nalowa ku chigwa cha Esikolo, nachizonda. Ndipo anatengako zipatso za dzikoli m'manja mwao, natsikira nazo kwa ife, natibwezera mau ndi kuti, Dzikoli Yehova Mulungu wathu atipatsa ndi labwino. Koma simunafuna kukwerako, ndipo munapikisana nao mau a Yehova Mulungu wanu. Ndipo munadandaula m'mahema mwanu, ndi kuti, Popeza anatida Yehova, Iye anatitulutsa m'dziko la Ejipito, kutipereka m'manja mwa Aamori, ationonge. Tikwere kuti? Abale athu atimyukitsa mitima yathu, ndi kuti, Anthuwo ndiwo akulu ndi atali akuposa ife; midzi ndi yaikulu ndi ya malinga ofikira m'mwamba: tinaonakonso ana a Anaki. Pamenepo ndinati kwa inu, Musamaopsedwa, musamachita mantha nao. Yehova Mulungu wanu wakutsogolera inu, Iye adzathirira inu nkhondo, monga mwa zonse anakuchitirani m'Ejipito pamaso panu; ndi kuchipululu, kumene munapenya kuti Yehova Mulungu wanu anakunyamulani, monga anyamula mwana wake wamwamuna, m'njira monse munayendamo, kufikira mutalowa m'malo muno. Koma m'chinthu ichi simunakhulupirira Yehova Mulungu wanu, amene anakutsogolerani m'njira, kukufunirani malo akumanga mahema anu ndi moto usiku, kukuonetserani njira yoyendamo inu, ndi mumtambo usana. Ndipo Yehova anamva mau a kunena kwanu, nakwiya, nalumbira, ndi kuti, Palibe mmodzi wa anthu awa a mbadwo uno woipa adzaona dziko lokomalo ndinalumbira kupatsa makolo anuli. Koma Kalebe mwana wa Yefune, iye adzaliona; ndidzampatsa iye dziko limene anapondapo, ndi ana ake; popeza analimbika ndi kutsata Yehova. Yehova anakwiya ndi inenso chifukwa cha inu, ndi kuti, Iwenso sudzalowamo. Yoswa mwana wa Nuni, wakuima pamaso pako, iye adzalowamo; umlimbitse mtima; popeza iye adzalandiritsa Israele. Ndipo ana anu amene mudanena, Adzakhala ogulidwa, ndi ana anu osadziwa chabwino kapena choipa ndi pano, iwo adzalowamo, ndidzawapatsa iwo ili, adzalilandira ndi iwo. Koma inu, bwererani, mukani ulendo wanu kuchipululu, njira ya ku Nyanja Yofiira. Pamenepo munayankha ndi kunena ndi ine, Tachimwira Yehova, tidzakwera ndi kuthira nkhondo monga mwa zonse Yehova Mulungu wathu atiuza. Ndipo munadzimangira munthu yense zida zake za nkhondo, nimunakonzeka kukwera kunka kumapiri. Koma Yehova anati kwa ine, Nena nao, Musakwerako, kapena kuthira nkhondo; popeza sindili pakati panu; angakukantheni adani anu. Pamene ndinanena ndi inu simunamvera; koma munatsutsana nao mau a Yehova ndi kuchita modzikuza, nimunakwera kunka kumapiri. Ndipo Aamori, akukhala m'mapiri muja, anatuluka kukomana ndi inu, nakupirikitsani, monga zimachita njuchi, nakukanthani m'Seiri, kufikira ku Horoma. Ndipo munabwerera ndi kulira pamaso pa Yehova; koma Yehova sanamvere mau anu, kapena kukutcherani khutu. Potero munakhala m'Kadesi masiku ambiri, monga mwa masiku munakhalako. Pamenepo tinabwerera, ndi kuyenda kunka kuchipululu, kutsata njira ya Nyanja Yofiira, monga Yehova adanena ndi ine; ndipo tinapaza phiri la Seiri masiku ambiri. Ndipo Yehova ananena ndi ine, ndi kuti, Yakwanira nthawi yakupaza inu phiri ili; tembenukani kunka kumpoto. Ndipo uuze anthu, ndi kuti, Mukapite kubzola malire a abale anu, ana a Esau okhala m'Seiri; ndipo adzakuopani; muchenjere ndithu; musalimbana nao; popeza sindikupatsakoni dziko lao, pangakhale popondapo phazi lanu ai; pakuti ndapatsa Esau phiri la Seiri likhale lakelake. Mugulane nao chakudya ndi ndalama, kuti mudye; mugulane naonso madzi kuti mumwe. Pakuti Yehova Mulungu wanu anakudalitsani mu ntchito zonse za manja anu; anadziwa kuyenda kwanu m'chipululu ichi chachikulu; zaka izi makumi anai Yehova Mulungu wanu anakhala ndi inu; simunasowa kanthu. Potero tinapitirira abale athu, ana a Esau okhala m'Seiri, njira ya chidikha, ku Elati ndi ku Eziyoni-Gebere. Pamenepo tinatembenuka ndi kudzera njira ya chipululu cha Mowabu. Ndipo Yehova anati kwa ine, Usavuta Mowabu, kapena kuutsana naye nkhondo; popeza sindidzakupatsako dziko lake likhale lakolako; pakuti ndinapatsa ana a Loti Ari likhale laolao. (Aemimu anakhalamo kale, ndiwo anthu akulu, ndi ambiri, ndi ataliatali, ngati Aanaki. Anawayesa iwonso Arefaimu, monga Aanaki; koma Amowabu awatcha Aemimu. Ndipo Ahori anakhala m'Seiri kale, koma ana a Esau analanda dziko lao, nawaononga pamaso pao, nakhala m'malo mwao; monga Israele anachitira dziko lakelake, limene Yehova anampatsa). Ukani tsopano, olokani mtsinje wa Zeredi. Ndipo tinaoloka mtsinje wa Zeredi. Ndipo masiku amene tinayenda kuchokera ku Kadesi-Baranea, kufikira tidaoloka mtsinje wa Zeredi, ndiwo zaka makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu; kufikira utatha mbadwo wonse wa amuna ankhondo m'chigono, monga Yehova adawalumbirira. Komanso dzanja la Yehova linatsutsana nao, kuwaononga m'chigono, kufikira adawatha. Ndipo kunali, atatha kufa amuna onse ankhondo mwa anthu, Yehova ananena ndi ine, ndi kuti, Lero lomwe utumphe malire a Mowabu, ndiwo Ari. Ndipo pamene uyandikiza popenyana ndi ana a Amoni, usawavuta, kapena kuutsana nao; popeza sindidzakupatsako dziko la ana a Amoni likhale lakolako; popeza ndinapatsa ana a Loti ili likhale laolao. (Ilinso aliyesa dziko la Arefaimu; Arefaimu anakhalamo kale; koma Aamoni awatcha Azamzumimu; ndiwo anthu akulu, ndi ambiri, ndi atalitali, monga Aanaki; koma Yehova anawaononga pamaso pao; ndipo analanda dziko lao, nakhala m'malo mwao; monga Iye anachitira ana a Esau, akukhala m'Seiri, pamene anaononga Ahori pamaso pao; ndipo analanda dziko lao, nakhala m'malo mwao kufikira lero lomwe. Kunena za Aavimu akukhala m'midzi kufikira ku Gaza, Akafitori, akufuma ku Kafitori, anawaononga, nakhala m'malo mwao). Uka, yenda ulendo wako, ndi kuoloka mtsinje wa Arinoni; taonani, ndapereka Sihoni mfumu ya Hesiboni, Mwamori, ndi dziko lake m'dzanja lako; yamba kulilandira, ndi kuutsana naye nkhondo. Tsiku lino ndiyamba kuopsetsa nawe ndi kuchititsa mantha nawe anthu a pansi pa thambo lonse, amene adzamva mbiri yako, nadzanjenjemera, nadzawawidwa chifukwa cha iwe. Ndipo ndinatuma amithenga ochokera ku chipululu cha Kedemoti kwa Sihoni mfumu ya Hesiboni ndi mau a mtendere, ndi kuti, Ndipitire m'dziko mwako; ndidzatsata mseu, osapatuka ine ku dzanja lamanja kapena kulamanzere, Undigulitse chakudya ndi ndalama, kuti ndidye; ndi kundipatsa madzi kwa ndalama, kuti ndimwe; chokhachi ndipitire choyenda pansi; monga anandichitira ana a Esau akukhala m'Seiri, ndi Amowabu akukhala m'Ari; kufikira nditaoloka Yordani kulowa dziko limene Yehova Mulungu wathu atipatsa. Koma Sihoni mfumu ya Hesiboni sanatilole kupitira kwao; popeza Yehova Mulungu wanu anaumitsa mzimu wake, nalimbitsa mtima wake, kuti ampereke m'dzanja lanu, monga lero lino. Ndipo Yehova anati kwa ine, Taona, ndayamba kupereka Sihoni ndi dziko lake pamaso pako; yamba kulandira dziko lake likhale lakolako. Pamenepo Sihoni anatuluka kukomana nafe, iye ndi anthu ake onse, kugwirana nafe nkhondo ku Yahazi. Ndipo Yehova Mulungu wathu anampereka iye pamaso pathu; ndipo tinamkantha, iye ndi ana ake amuna ndi anthu ake onse. Ndipo muja tinalanda midzi yake yonse; ndipo tinaononga konse midzi yonse, amuna ndi akazi ndi ana; sitinasiyapo ndi mmodzi yense. Zoweta zokha tinadzifunkhira, pamodzi ndi zofunkha za midzi tidailanda. Kuyambira ku Aroere, ndiko kumphepete kwa mtsinje wa Arinoni, ndi kumudzi wokhala kumtsinje kufikira ku Giliyadi, kunalibe mudzi wakutitalikira malinga ake; Yehova Mulungu wathu anapereka yonse pamaso pathu. Ku dziko la ana a Amoni lokha simunayandikiza; dera lonse la mtsinje wa Yaboki, ndi midzi ya kumapiri, ndi kwina kulikonse Yehova Mulungu wathu anatiletsa. Pamenepo tinatembenuka, ndi kubwera kunka njira ya ku Basani; ndipo Ogi mfumu ya Basani anatuluka kukomana nafe, kugwirana nafe nkhondo, iye ndi anthu ake onse, ku Ederei. Ndipo Yehova anati kwa ine, Usamuopa; popeza ndampereka iye ndi anthu ake onse, ndi dziko lake, m'dzanja lako; umchitire monga umo unachitira Sihoni mfumu ya Aamori, amene anakhala m'Hesiboni. Potero Yehova Mulungu wathu anaperekanso m'manja mwathu Ogi mfumu ya Basani, ndi anthu ake onse, ndipo tinamkantha kufikira sanamtsalire ndi mmodzi yense. Ndipo muja tinalanda midzi yake yonse; kunalibe mudzi sitinaulanda m'manja mwao, midzi makumi asanu ndi limodzi, dera lonse la Arigobu, dziko la Ogi m'Basani. Yonseyi ndiyo midzi yozinga ndi malinga atali, zitseko, ndi mipiringidzo; pamodzi ndi midzi yambirimbiri yopanda malinga. Ndipo tinaiononga konse, monga umo tinachitira Sihoni mfumu ya Hesiboni, ndi kuononga konse midzi yonse, amuna, akazi ndi ana. Koma zoweta zonse ndi zofunkha za m'midzi, tinadzifunkhira tokha. Ndipo muja tinalanda dziko m'manja mwa mafumu awiri a Aamori okhala tsidya lija la Yordani, kuyambira mtsinje wa Arinoni kufikira phiri la Heremoni; (Asidoni alitcha Heremoni Sirioni, koma Aamori alitcha Seniri); midzi yonse ya kuchidikha, ndi Giliyadi lonse, ndi Basani lonse kufikira ku Saleka ndi Ederei, midzi ya dziko la Ogi m'Basani. (Pakuti Ogi mfumu ya Basani anatsala yekha wa iwo otsalira Arefaimu; taonani, kama wake ndiye kama wachitsulo; sukhala kodi m'Raba wa ana a Amoni? Utali wake mikono isanu ndi inai, kupingasa kwake mikono inai, kuyesa mkono wa munthu). Ndipo dziko ili tinalilanda muja; kuyambira ku Aroere, wa ku mtsinje wa Arinoni, ndi dera lina la ku mapiri a Giliyadi, ndi midzi yake, ndinapatsa Arubeni ndi Agadi. Ndi chotsalira cha Giliyadi, ndi Basani lonse, dziko la Ogi, ndinapatsa fuko la hafu la Manase; dziko lonse la Arigobu, pamodzi ndi Basani. (Ndilo lotchedwa dziko la Arefaimu. Yairi mwana wa Manase analanda dziko lonse la Arigobu, kufikira malire a Agesuri ndi Amaakati; nalitcha dzina lake, Basani Havoti-Yairi, kufikira lero lino). Ndipo ndinampatsa Makiri Giliyadi. Koma ndinapatsa Arubeni ndi Agadi kuyambira ku Giliyadi kufikira ku mtsinje wa Arinoni, pakati pa chigwa ndi malire ake, kufikira mtsinje wa Yaboki, ndiwo malire a ana a Amoni; ndi chidikha, ndi Yordani ndi malire ake, kuyambira ku Kinereti kufikira ku Nyanja ya Araba, ndiyo Nyanja ya Mchere, patsinde pa Pisiga, kum'mawa. Ndipo ndinauza inu muja, ndi kuti, Yehova Mulungu wanu wakupatsani dziko ili likhale lanulanu, muoloke, amuna onse amphamvu ovala zida zao, pamaso pa abale anu ana a Israele. Koma akazi anu, ndi ana anu, ndi zoweta zanu, (ndidziwa muli nazo zoweta zambiri), zikhale m'midzi yanu imene ndinakupatsani; kufikira Yehova atapumulitsa abale anu, monga anapumulitsa inu, nalandira iwonso dziko limene Yehova Mulungu wanu awapatsa tsidya lija la Yordani; pamenepo mudzabwerera munthu yense ku cholowa chake, chimene ndinakupatsani. Ndipo ndinauza Yoswa muja, ndi kuti, Maso ako anapenya zonse Yehova Mulungu wanu anawachitira mafumu awa awiri; momwemo Yehova adzachitira maufumu onse kumene muolokerako. Musawaopa popeza Yehova Mulungu wanu, ndiye agwirira inu nkhondo. Ndipo ndinapempha chifundo kwa Yehova nthawi yomwe ija, ndi kuti, Ambuye Yehova, mwayamba Inu kuonetsera mtumiki wanu ukulu wanu, ndi dzanja lanu lamphamvu; pakuti Mulungu ndani m'mwamba kapena pa dziko lapansi wakuchita monga mwa ntchito zanu, ndi monga mwa mphamvu zanu? Ndioloketu, ndilione dziko lokomali lili tsidya la Yordani, mapiri okoma aja, ndi Lebanoni. Koma Yehova anakwiya ndi ine, chifukwa cha inu, sanandimvere ine; ndipo Yehova anati kwa ine, Chikukwanire, usaonjezenso kunena ndi Ine za chinthuchi. Kwera kumwamba ku Pisiga, nukweze maso ako kumadzulo, ndi kumpoto, ndi kumwera, ndi kum'mawa, nuyang'ane ndi maso ako; popeza sudzaoloka Yordani uyo. Koma langiza Yoswa, numlimbitse mtima, ndi kumkhwimitsa, pakuti adzaoloka pamaso pa anthu awa, nadzawalandiritsa dziko ulionali likhale laolao. Potero tinakhala m'chigwamo pandunji pa Betepeori. Ndipo tsopano, Israele, tamverani malemba ndi maweruzo, amene ndikuphunzitsani muwachite; kuti mukhale ndi moyo, ndi kulowa, ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu akupatsani. Musamaonjeza pa mau amene ndikuuzani, kapena kuchotsapo, kuti musunge malamulo a Yehova Mulungu wanu, amene ndikuuzani. Maso anu anapenya chochita Yehova chifukwa cha Baala-Peori; pakuti amuna onse amene anatsata Baala-Peori, Yehova Mulungu wanu anawaononga pakati panu. Koma inu amene munamamatira Yehova Mulungu wanu muli ndi moyo nonsenu lero lomwe. Taonani, ndinakuphunzitsani malemba ndi maweruzo, monga Yehova Mulungu wanga anandiuza ine, kuti muzichita chotero pakati pa dziko limene mumkako kulilandira likhale lanulanu. Chifukwa chake asungeni, achiteni; pakuti ichi ndi nzeru zanu ndi chidziwitso chanu pamaso pa mitundu ya anthu akumva malemba ndi kuti, Ndithu mtundu waukulu uwu, ndiwo athu anzeru ndi akuzindikira. Pakuti mtundu waukulu wa anthu ndi uti, wakukhala ndi Mulungu pafupi pao monga amakhala Yehova Mulungu wathu, pamene paliponse timaitanira Iye? Ndipo mtundu waukulu wa anthu ndi uti, wakukhala nao malemba ndi maweruzo olungama, akunga chilamulo ichi chonse ndichiika pamaso panu lero lino? Chokhachi, dzichenjerani nokha, ndi kusunga moyo wanu mwachangu, kuti mungaiwale zinthuzi adaziona maso anu, ndi kuti zisachoke kumtima kwanu masiku onse a moyo wanu; koma muzidziwitsa ana anu ndi zidzukulu zanu. Tsikuli munaima pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'Horebu muja Yehova anati kwa ine, Ndisonkhanitsire anthu, ndidzawamvetsa mau anga, kuti aphunzire kundiopa Ine masiku ao onse akukhala ndi moyo pa dziko lapansi, ndi kuti aphunzitse ana ao. Ndipo munayandikiza ndi kuima patsinde pa phiri; ndi phirilo linayaka moto kufikira pakati pa thambo; kunali mdima, ndi mtambo, inde mdima bii. Pamenepo Yehova ananena ndi inu ali pakati pa moto; munamva kunena kwa mau, osaona maonekedwe, koma kunenako. Pamenepo anakufotokozerani chipangano chake, chimene anakulamulirani kuchichita, ndiwo Mau Khumi; nawalemba pa magome awiri amiyala. Ndipo Yehova anandilamulira muja ndikuphunzitseni malemba ndi maweruzo, kuti mukawachite m'dziko limene muolokerako kulilandira likhale lanulanu. Potero dzichenjerani nao moyo wanu ndithu; popeza simunapenya mafanidwe konse tsikuli Yehova ananena ndi inu m'Horebu, ali pakati pa moto; kuti mungadziipse, ndi kudzipangira fano losema, lakunga chifaniziro chilichonse, mafanidwe a mwamuna kapena mkazi; mafanidwe a nyama iliyonse ili pa dziko lapansi, mafanidwe a mbalame iliyonse yamapiko yakuuluka m'mlengalenga, mafanidwe a chinthu chilichonse chokwawa pansi, mafanidwe a nsomba iliyonse yokhala m'madzi pansi pa dziko; ndi kuti mungakweze maso anu kupenya kumwamba, ndipo poona dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi, khamu lonse la kumwamba, munganyengedwe ndi kuzigwadira, ndi kuzitumikira, zimene Yehova Mulungu wanu anagawira mitundu yonse ya anthu pansi pa thambo lonse. Koma Yehova anakutengani, nakutulutsani m'ng'anjo yamoto, m'Ejipito, mukhale kwa Iye anthu a cholowa chake, monga mukhala lero lino. Yehova anakwiyanso nane chifukwa cha mau anu, nalumbira kuti sindidzaoloka Yordani ine, ndi kuti sindidzalowa m'dziko lokomali Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanu; pakuti ndidzafa m'dziko muno, osaoloka Yordani; koma inu mudzaoloka, ndi kulandira dziko ili lokoma likhale lanulanu. Dzichenjerani, mungaiwale chipangano cha Yehova Mulungu wanu, chimene anapangana nanu, ndi kuti mungadzipangire fano losema, chifaniziro cha kanthu kalikonse Yehova Mulungu wanu anakuletsani. Pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye moto wonyeketsa, ndi Mulungu wansanje. Mutakabala ana, ndi zidzukulu, ndipo mutakakhala nthawi yaikulu m'dzikomo, ndi kudziipsa, ndi kupanga fano losema, m'chifaniziro cha kanthu kalikonse, ndi kuchita choipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wake: ndiitana kumwamba ndi dziko lapansi zichite mboni pa inu lero lino, kuti mudzaonongeka msangatu kuchotsedwa ku dziko limene muolokera Yordani kulilandira likhale lanulanu; masiku anu sadzachuluka pamenepo, koma mudzaonongeka konse. Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu ya anthu, nimudzatsala pang'ono mwa amitundu, kumene Yehova adzakutsogolerani kwao. Ndipo kumeneko mudzatumikira milungu, ntchito ya manja a anthu, mtengo ndi mwala, yosapenya, kapena kumva, kapena kudya, kapena kununkhiza. Koma mukafuna Yehova Mulungu wanu kumeneko, mudzampeza, ngati mumfunafuna ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse. Mukakhala nao msauko, zikakugwerani zonsezi, masiku otsiriza mudzabwerera kwa Yehova Mulungu wanu ndi kumvera mau ake; popeza Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wachifundo; sadzakusiyani, kapena kukuonongani, kapena kuiwala chipangano cha makolo anu chimene analumbirira iwo. Pakuti, funsiranitu, masiku adapitawo, musanakhale inu, kuyambira tsikuli Mulungu analenga munthu pa dziko lapansi, ndi kuyambira malekezero ena a thambo kufikira malekezero anzake a thambo, ngati chinthu chachikulu chonga ichi chinamveka, kapena kuchitika? Kodi pali mtundu wa anthu udamva mau a mulungu wina akunena pakati pa moto, monga mudamva inu, ndi kukhala ndi moyo? Kapena kodi anayesa Mulungu kumuka ndi kudzitengera mtundu mwa mtundu wina wa anthu, ndi mayesero, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi nkhondo, ndi mwa dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mwa zoopsa zachikulu, monga mwa zonse Yehova Mulungu wanu anakuchitirani m'Ejipito pamaso panu? Inu munachiona ichi, kuti mudziwe kuti Yehova ndiye Mulungu; palibe wina wopanda Iye. Anakumvetsani mau ake kuchokera kumwamba, kuti akuphunzitseni; ndipo pa dziko lapansi anakuonetsani moto wake waukulu; nimunamva mau ake pakati pa moto. Ndipo popeza anakonda makolo anu, anasankha mbeu zao zakuwatsata, nakutulutsani pamaso pake ndi mphamvu yake yaikulu, m'Ejipito; kupirikitsa amitundu akulu ndi amphamvu oposa inu pamaso panu, kukulowetsani ndi kukupatsani dziko lao likhale cholowa chanu, monga lero lino. Potero dziwani lero lino nimukumbukire m'mtima mwanu, kuti Yehova ndiye Mulungu, m'thambo la kumwamba ndi pa dziko lapansi; palibe wina. Muzisunga malemba ake, ndi malamulo ake, amene ndikuuzani lero lino, kuti chikukomereni inu ndi ana anu akukutsatani, ndi kuti masiku anu achuluke pa dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanu kosatha. Pamenepo Mose anapatula midzi itatu tsidya lija la Yordani lotuluka dzuwa; kuti athawireko wakupha munthu, osamupha mnansi wake dala, osamkwiyira ndi kale lonse; ndi kuti, akathawira ku umodzi wa midzi iyi, akhale ndi moyo: ndiyo Bezeri, m'chipululu, m'dziko lachidikha, ndiwo wa Arubeni; ndi Ramoti m'Giliyadi, ndiwo wa Agadi; ndi Golani, m'Basani, ndiwo wa Amanase. Ndipo ichi ndi chilamulo Mose anachiika pamaso pa ana a Israele; izi ndi mboni, ndi malemba, ndi maweruzo, Mose anazinena kwa ana a Israele, potuluka iwo m'Ejipito; tsidya lija la Yordani, m'chigwa cha pandunji pa Betepeori, m'dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, wakukhala m'Hesiboni, amene Mose ndi ana a Israele anamkantha, potuluka iwo m'Ejipito; ndipo analanda dziko lake, ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani, mafumu awiri a Aamori, akukhala tsidya lija la Yordani lotuluka dzuwa; kuyambira ku Aroere, ndiwo m'mphepete mwa mtsinje wa Arinoni, kufikira phiri la Sirioni (ndilo Heremoni), ndi chidikha chonse tsidya lija la Yordani kum'mawa, kufikira ku Nyanja ya Araba, pa tsinde lake la Pisiga. Ndipo Mose anaitana Israele wonse, nanena nao, Tamverani, Israele, malemba ndi maweruzo ndinenawa m'makutu mwanu lero, kuti muwaphunzire, ndi kusamalira kuwachita. Yehova Mulungu wathu anapangana nafe chipangano m'Horebu. Yehova sanachite chipangano ichi ndi makolo athu, koma ndi ife, ife amene tili ndi moyo tonsefe pano lero. Yehova ananena ndi inu popenyana maso m'phirimo, ali pakati pa moto, (ndinalinkuima pakati pa Yehova ndi inu muja, kukulalikirani mau a Yehova; popeza munachita mantha chifukwa cha moto, osakwera m'phirimo) ndi kuti: Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakutulutsa m'dziko la Ejipito, m'nyumba ya akapolo. Usakhale nayo milungu ina koma Ine ndekha. Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m'thambo la kumwamba, kapena za m'dziko lapansi, kapena za m'madzi a pansi pa dziko; usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndine Mulungu wansanje, wakulanga ana chifukwa cha atate wao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai wa iwo amene akudana ndi Ine; ndi kuchitira chifundo anthu zikwi, a iwo amene akondana ndi Ine nasunga malamulo anga. Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe; chifukwa Yehova sadzamuyesa iye wosachimwa amene atchula pachabe dzina lakelo. Samalira tsiku la Sabata likhale lopatulika, monga Yehova Mulungu wako anakulamulira. Masiku asanu ndi limodzi uzigwiritsa ntchito, ndi kuchita ntchito zako zonse; koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata la Yehova Mulungu wako; usamagwira ntchito iliyonse, iwe, kapena mwana wako wamwamuna, kapena mwana wako wamkazi, kapena wantchito wako wamwamuna, kapena wantchito wako wamkazi, kapena ng'ombe yako, kapena bulu wako, kapena zoweta zako zilizonse, kapena mlendo wokhala m'mudzi mwako; kuti wantchito wako wamwamuna ndi wantchito wako wamkazi apumule monga iwe mwini. Ndipo uzikumbukira kuti unali kapolo m'dziko la Ejipito, ndi kuti Yehova Mulungu wako anakutulutsako ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasuka; chifukwa chake Yehova Mulungu wako anakulamulira kusunga tsiku la Sabata. Lemekeza atate wako ndi amai ako, monga Yehova Mulungu wako anakulamulira; kuti masiku ako achuluke, ndi kuti chikukomere, m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe. Usaphe. Usachite chigololo. Usabe. Usamnamizire mnzako. Usasirire mkazi wake wa mnzako; usakhumbe nyumba yake ya mnzako, munda wake, kapena wantchito wake wamwamuna, kapena wantchito wake wamkazi, ng'ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako. Yehova ananena mau awa kwa msonkhano wanu wonse, m'phirimo ali pakati pa moto, pamtambo, pamdima bii, ndi mau akulu; osaonjezapo kanthu. Ndipo anawalembera pa magome awiri amiyala, nandipatsa awa. Ndipo kunali, pamene munamva liu lotuluka pakati pa mdima, potentha phiri ndi moto, munayandikiza kwa ine, ndiwo mafumu onse a mafuko anu ndi akulu anu; ndipo munati, Taonani, Yehova Mulungu wathu anationetsa ulemerero wake, ndi ukulu wake, ndipo tidamva liu lake ali pakati pa moto; tapenya lero lino kuti Mulungu anena ndi munthu, ndipo akhala ndi moyo. Ndipo tsopano tiferenji? Popeza moto waukulu uwu udzatitha. Tikaonjeza kumva mau a Yehova Mulungu wathu, tidzafa. Pakuti ndaniyo, wa zamoyo zonse adamva mau a Mulungu wamoyo wakunena ali pakati pa moto, monga ife nakhala ndi moyo? Yandikizani inu, ndi kumva zonse Yehova Mulungu wathu adzati; ndipo inu munene ndi ife zonse zimene Yehova Mulungu wathu adzanena ndi inu; ndipo ife tidzazimva ndi kuzichita. Ndipo Yehova anamva mau a kunena kwanu, pamene munanena ndi ine; ndipo Yehova anati kwa ine, Ndidamva mau a kunena kwao kwa anthu awa, amene ananena ndi iwe; chokoma chokhachokha adanenachi. Ha? Mwenzi akadakhala nao mtima wotere wakundiopa Ine, ndi kusunga malamulo anga masiku onse, kuti chiwakomere iwo ndi ana ao nthawi zonse! Muka, nuti nao, Bwererani ku mahema anu. Koma iwe, uime kuno ndi Ine, ndinene ndi iwe malamulo onse, ndi malamba, ndi maweruzo, amene uziwaphunzitsa, kuti awachite m'dziko limene ndiwapatsa likhale laolao. Potero muzisamalira kuchita monga Yehova Mulungu wanu anakulamulirani; musamapatuka kulamanzere kapena kulamanja. Muziyenda m'njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani, kuti mukakhale ndi moyo, ndi kuti chikukomereni, ndi kuti masiku anu achuluke m'dziko limene mudzakhala nalo lanulanu. Ndipo awa ndi malamulo, malemba, ndi maweruzo, amene Yehova Mulungu wanu analamulira kukuphunzitsani, kuti muziwachita m'dziko limene muolokerako kulilandira; kuti muope Yehova Mulungu wanu, kusunga malemba ake onse ndi malamulo ake, amene ndikuuzani inu ndi ana anu, ndi zidzukulu zanu, masiku onse a moyo wanu, ndi kuti masiku anu achuluke. Potero imvani, Israele, musamalire kuwachita, kuti chikukomereni ndi kuti muchuluke chichulukire, monga Yehova Mulungu wa makolo anu anena ndi inu, m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi. Imvani, Israele; Yehova Mulungu wathu, Yehova ndiye mmodzi; ndipo muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse. Ndipo mau awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu; ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m'nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu. Ndipo muziwamanga padzanja panu ngati chizindikiro, ndipo akhale ngati chapamphumi pakati pa maso anu. Ndipo muziwalembera pa mphuthu za nyumba zanu, ndi pa zipata zanu. Ndipo kudzakhala, Yehova Mulungu wanu atakulowetsani m'dziko limene analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, kuti adzakupatsani ili; midzi yaikulu ndi yokoma, imene simunaimanga; ndi nyumba zodzala nazo zokoma zilizonse, zimene simunazidzaza, ndi zitsime zosema, zimene simunazisema, minda yampesa, ndi minda ya azitona, zimene simunazioka, ndipo mutakadya ndi kukhuta; pamenepo mudzichenjere mungaiwale Yehova, amene anakutulutsani m'dziko la Ejipito, m'nyumba ya akapolo. Muziopa Yehova Mulungu wanu; ndi kutumikira Iyeyu; ndipo polumbira muzitchula dzina lake. Musamatsata milungu ina, milungu ina ya mitundu ya anthu akuzinga inu; pakuti Yehova Mulungu wanu ali pakati panu, ndiye Mulungu wansanje; kuti ungapse mtima wa Yehova Mulungu wanu, ndi kukuonongani, kukuchotsani pankhope pa dziko lapansi. Musamayesa Yehova Mulungu wanu, monga munamyesa m'Masa. Muzisunga mwachangu malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi mboni zake, ndi malemba ake, amene anakulamulirani. Ndipo muzichita zolunjika ndi zokoma pamaso pa Yehova; kuti chikukomereni, ndi kuti mulowe kukalandira dziko lokomali Yehova analumbirira makolo anu, kuingitsa adani anu onse pamaso panu, monga Yehova adanena. Akakufunsani ana anu m'tsogolomo, ndi kuti, Mbonizo, ndi malemba, ndi maweruzo, zimene Yehova Mulungu wathu anakulamulirani, zitani? Pamenepo muzinena kwa ana anu, Tinali akapolo a Farao m'Ejipito; ndipo Yehova anatitulutsa m'Ejipito ndi dzanja lamphamvu. Ndipo Yehova anapatsa zizindikiro ndi zozizwa zazikulu ndi zowawa m'Ejipito, pa Farao, ndi pa nyumba yake yonse, pamaso pathu; ndipo anatitulutsa komweko, kuti atilowetse, kutipatsa dzikoli analumbirira makolo athu. Ndipo Yehova anatilamulira tizichita malemba awa onse, kuopa Yehova Mulungu wathu, kuti tipindule nako masiku onse, kuti atisunge amoyo, monga lero lino. Ndipo kudzakhala kwa ife chilungamo, ngati tisamalira kuchita malamulo awa onse pamaso pa Yehova Mulungu wathu, monga anatilamulira ife. Pamene Yehova Mulungu wanu atakulowetsani m'dziko limene mumkako kulilandira likhale lanulanu, ndipo atakataya amitundu ambiri pamaso panu, Ahiti, ndi Agirigasi, ndi Aamori, ndi Akanani, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, mitundu isanu ndi iwiri yaikulu ndi yamphamvu yoposa inu; nakawapereka Yehova Mulungu wanu pamaso panu, ndipo mukawakanthe; pamenepo muwaononge konse; musapangana nao pangano, kapena kuwachitira chifundo. Ndipo musakwatitsane nao; musampatse mwana wake wamwamuna mwana wanu wamkazi, kapena kutenga mwana wake wamkazi akhale wa mwana wanu wamwamuna. Popeza adzapatutsa mwana wanu aleke kunditsata Ine, kuti atumikire milungu ina; potero Yehova adzapsa mtima pa inu, ndipo adzakuonongani msanga. Koma muzichita nao motero: mukapasule maguwa ao a nsembe, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kulikha zifanizo zao, ndi kutentha mafano ao osema ndi moto. Pakuti inu ndinu mtundu wa anthu wopatulika wa Yehova Mulungu wanu; Yehova Mulungu wanu anakusankhani, mukhale mtundu wa pa wokha wa Iye yekha, mwa mitundu yonse ya anthu akukhala pa nkhope ya dziko. Yehova sanakondwere nanu, ndi kukusankhani chifukwa cha kuchuluka kwanu koposa mitundu yonse ina ya anthu, kapena kuchepera kwanu; koma Yehova anakutulutsani ndi dzanja lamphamvu, ndi kukuombolani m'nyumba ya akapolo, m'dzanja la Farao mfumu ya Aejipito, chifukwa Yehova akukondani, ndi chifukwa cha kusunga lumbiro lija analumbirira makolo anu. Chifukwa chake dziwani kuti Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu; ndiye Mulungu wokhulupirika, wakusunga chipangano ndi chifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ake, kufikira mibadwo zikwi. Ndipo awabwezera onse akudana ndi Iye, pamaso pao, kuwaononga; sachedwa naye wakudana ndi Iye, ambwezera pamaso pake. Potero muzisunga malamulo, ndi malemba, ndi maweruzo amene ndikuuzani lero kuwachita. Ndipo kudzakhala, chifukwa cha kumvera inu maweruzo awa, ndi kuwasunga, ndi kuwachita, Yehova Mulungu wanu adzakusungirani chipangano ndi chifundo chimene analumbirira makolo anu; ndipo adzakukondani, ndi kukudalitsani, ndi kukuchulukitsani; adzadalitsanso zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, tirigu wanu, ndi vinyo wanu, ndi mafuta anu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi anaankhosa anu, m'dziko limene analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani. Mudzakhala odalitsika koposa mitundu yonse ya anthu; sipadzakhala mwamuna kapena wamkazi wosabala pakati pa inu, kapena pakati pa zoweta zanu. Ndipo Yehova adzakuchotserani nthenda zonse; sadzakuikirani nthenda zoipa zilizonse za Aejipito muzidziwa zija; koma adzaziika pa onse akudana ndi inu. Ndipo mudzatha mitundu yonse ya anthu amene Yehova Mulungu wanu adzapereka kwa inu; diso lanu lisawachitire chifundo; musamatumikira milungu yao; pakuti uku kudzakuchitirani msampha. Mukadzanena m'mtima mwanu, Amitundu awa andichulukira; ndikhoza bwanji kuwapirikitsa? Musamawaopa; mukumbukire bwino chimene Yehova Mulungu wanu anachitira Farao, ndi Ejipito wonse; mayesero akulu maso anu anawapenya, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, zimene Yehova Mulungu wanu anakutulutsani nazo; Yehova Mulungu wanu adzatero nayo mitundu yonse ya anthu imene muwaopa. Komanso Yehova Mulungu wanu adzatumiza mavu pakati pao, kufikira ataonongeka otsalawo, ndi akubisala pamaso panu. Musamaopa pamaso pao; popeza Yehova Mulungu wanu ali pakati pa inu, Mulungu wamkulu ndi woopsa. Ndipo Yehova Mulungu wanu adzataya amitundu awa pang'onopang'ono; simuyenera kuwaononga msanga, kuti zingakuchulukireni zilombo. Koma Yehova Mulungu wanu adzawapereka pamaso panu, nadzawapirikitsa ndi kupirikitsa kwakukulu, kufikira ataonongeka. Adzaperekanso mafumu ao m'dzanja mwanu, ndipo muwafafanize maina ao pansi pa thambo; palibe munthu mmodzi adzaima pamaso panu, kufikira mutawaononga. Mafano osema a milungu yao muwatenthe ndi moto; musamasirira siliva ndi golide zili pa iwo, kapena kudzitengera izi; mungakodwe nazo; pakuti izi zinyansira Yehova Mulungu wanu. Musamalowa nacho chonyansachi m'nyumba mwanu, kuti mungaonongeke konse pamodzi nacho; muziipidwa nacho konse, ndi kunyansidwa nacho konse; popeza ndi chinthu choyenera kuonongeka konse. Muzisamalira kuchita malamulo onse amene ndikuuzani lero lino, kuti mukhale ndi moyo, ndi kuchuluka, ndi kulowa, ndi kulandira dziko limene Yehova analumbirira makolo anu. Ndipo mukumbukire njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakuyendetsani m'chipululu zaka izi makumi anai, kuti akuchepetseni, kukuyesani, kudziwa chokhala mumtima mwanu, ngati mudzasunga malamulo ake, kapena iai. Ndipo anakuchepetsani, nakumvetsani njala, nakudyetsani ndi mana, amene simunawadziwe, angakhale makolo anu sanawadziwe; kuti akudziwitseni kuti munthu sakhala wamoyo ndi mkate wokha, koma munthu akhala wamoyo ndi zonse zakutuluka m'kamwa mwa Yehova. Zovala zanu sizinatha pathupi panu, phazi lanu silinatupa zaka izi makumi anai. Ndipo muzindikire m'mtima mwanu, kuti monga munthu alanga mwana wake, momwemo Yehova Mulungu wanu akulangani inu. Ndipo muzisunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zake, ndi kumuopa. Pakuti Yehova Mulungu wanu akulowetsani m'dziko lokoma, dziko la mitsinje yamadzi, la akasupe ndi la maiwe akutuluka m'zigwa, ndi m'mapiri; dziko la tirigu ndi barele, ndi mipesa, ndi mikuyu, ndi makangaza; dziko la azitona a mafuta, ndi uchi; dziko loti mudzadyamo mkate wosapereweza; simudzasowamo kanthu; dziko loti miyala yake nja chitsulo, ndi m'mapiri ake mukumbe mkuwa. Ndipo mudzadya ndi kukhuta, ndi kuyamika Yehova Mulungu wanu chifukwa cha dziko lokomali anakupatsani. Chenjerani mungaiwale Yehova Mulungu wanu, ndi kusasunga malamulo ake, ndi maweruzo ake, ndi malemba ake, amene ndikuuzani lero lino; kuti, mutadya ndi kukhuta, ndi kumanga nyumba zokoma, ndi kukhalamo; ndipo zitachuluka ng'ombe zanu, ndi nkhosa zanu, zitachulukanso siliva wanu ndi golide wanu, zitachulukanso zonse muli nazo; mtima wanu ungatukumuke, nimungaiwale Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani m'dziko la Ejipito, m'nyumba ya akapolo; amene anakutsogolerani m'chipululu chachikulu ndi choopsacho, munali njoka zamoto, ndi zinkhanira, mouma mopanda madzi; amene anakutulutsirani madzi m'thanthwe lansangalabwi; amene anakudyetsani m'chipululu ndi mana, amene makolo anu sanawadziwe; kuti akuchepetseni, ndi kuti akuyeseni, kuti akuchitireni chokoma potsiriza panu; ndipo munganene m'mtima mwanu, Mphamvu yanga ndi mkono wanga wolimba zinandifunira chuma ichi. Koma mukumbukire Yehova Mulungu wanu, popeza ndi Iyeyu wakupatsani mphamvu yakuonera chuma; kuti akhazikitse chipangano chake chimene analumbirira makolo anu, monga chikhala lero lino. Ndipo kudzakhala kuti mukaiwalatu Yehova Mulungu wanu, ndi kutsata milungu ina ndi kuitumikira, ndikuchitirani mboni lero lino kuti mudzaonongeka ndithu. Monga amitundu amene Yehova awaononga pamaso panu, momwemo mudzaonongeka; chifukwa cha kusamvera mau a Yehova Mulungu wanu. Imvani Israele; mulikuoloka Yordani lero lino, kulowa ndi kulandira amitundu akulu ndi amphamvu akuposa inu, midzi yaikulu ndi ya malinga ofikira kuthambo, anthu akulu ndi atalitali, ana a Aanaki, amene muwadziwa, amene munamva mbiri yao, ndi kuti, Adzaima ndani pamaso pa ana a Anaki? Potero mudziwe lero lino, kuti Yehova Mulungu wanu ndiye amene aoloka pamaso panu ngati moto wonyeketsa; Iye adzawaononga, Iye adzawagwetsa pamaso panu; potero mudzawapirikitsa, ndi kuwaononga msanga, monga Yehova analankhula ndi inu. Musamanena mumtima mwanu, atawapirikitsa pamaso panu Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Chifukwa cha chilungamo changa Yehova anandilowetsa kudzalandira dziko ili; pakuti Yehova awapirikitsa pamaso panu chifukwa cha zoipa za amitundu awa. Simulowa kulandira dziko lao chifukwa cha chilungamo chanu, kapena mtima wanu woongoka; koma Yehova Mulungu wanu awapirikitsa pamaso panu chifukwa cha zoipa za amitundu awa, ndi kuti akhazikitse mau amene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo. Potero mudziwe, kuti Yehova Mulungu wanu sakupatsani dziko ili lokoma mulilandire, chifukwa cha chilungamo chanu; pakuti inu ndinu mtundu wa anthu opulukira. Kumbukirani, musamaiwala, kuti munakwiyitsa Yehova Mulungu wanu m'chipululu; kuyambira tsikuli munatuluka m'dziko la Ejipito, kufikira munalowa m'malo muno munapikisana ndi Yehova. M'Horebu momwe munautsa mkwiyo wa Yehova; ndipo Yehova anakwiya nanu kukuonongani. Muja ndinakwera m'phiri kukalandira magome amiyala, ndiwo magome a chipangano chimene Yehova anapangana ndi inu, ndinakhala m'phiri masiku makumi anai usana ndi usiku; osadya mkate osamwa madzi. Ndipo Yehova anapereka kwa ine magome awiri amiyala, olembedwa ndi chala cha Mulungu; ndipo panalembedwa pamenepo monga mwa mau onse amene Yehova adanena ndi inu m'phirimo, ali pakati pa moto, tsiku lakusonkhana. Ndipo kunali, atatha masiku makumi anai usana ndi usiku, kuti Yehova anandipatsa magome awiriwo amiyala, ndiwo magome a chipangano. Ndipo Yehova anati kwa ine, Uka, fulumira kutsika kuno popeza anthu ako unawatulutsa m'Ejipitowa anadziipsa; anapatuka msanga m'njira ndinawalamulirayi; anadzipangira fano loyenga. Yehova ananenanso ndi ine, ndi kuti, Ndapenya anthu awa, taona, awa ndi anthu opulukira; undileke, ndiwaononge, ndi kufafaniza dzina lao pansi pa thambo; ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu wa anthu wamphamvu ndi waukulu woposa iwo. Pamenepo ndinatembenuka ndi kutsika m'phiri, ndi phirilo linatentha ndi moto; ndi magome awiri a chipangano anali m'manja mwanga. Ndipo ndinapenya, taonani, mudachimwira Yehova Mulungu wanu; mudadzipangira mwanawang'ombe woyenga; mudapatuka msanga m'njira imene Yehova adalamulira inu. Pamenepo ndinagwira magome awiriwo, ndi kuwataya achoke m'manja anga awiri, ndi kuwaswa pamaso panu. Ndipo ndinagwa pansi pamaso pa Yehova, monga poyamba paja, masiku makumi anai usana ndi usiku, osadya mkate osamwa madzi, chifukwa cha machimo anu onse mudachimwa, ndi kuchita choipacho pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wake. Pakuti ndinachita mantha chifukwa cha mkwiyo waukali, umene Yehova anakwiya nao pa inu kukuonongani. Koma Yehova anandimvera nthawi ijanso. Ndipo Yehova anakwiya kwambiri ndi Aroni kumuononga; koma ndinampempherera Aroni nthawi yomweyo. Ndipo ndinatenga tchimo lanu, mwanawang'ombe mudampangayo, ndi mumtentha ndi moto, ndi kumphwanya, ndi kumpera bwino kufikira atasalala ngati fumbi; ndipo ndinataya fumbi lake m'mtsinje wotsika m'phirimo. Ku Tabera, ndi ku Masa, ndi ku Kibroti-Hatava, munautsanso mkwiyo wa Yehova. Ndipo pamene Yehova anakutumizani kuchokera ku Kadesi-Baranea, ndi kuti Kwerani, landirani dziko limene ndakupatsani; munapikisana nao mau a Yehova Mulungu wanu, osamkhulupirira, kapena kumvera mau ake. Munakhala opikisana ndi Yehova kuyambira tsikuli ndinakudziwani. Ndipo ndinagwa pansi pamaso pa Yehova masiku makumi anai usana ndi usiku ndinagwa pansiwa; popeza Yehova adati kuti adzakuonongani. Ndipo ndinapemphera kwa Yehova ndi kuti, Yehova Mulungu, musaononga anthu anu ndi cholowa chanu, amene mudawaombola mwa ukulu wanu, amene munawatulutsa m'Ejipito ndi dzanja lamphamvu. Kumbukirani atumiki anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo; musapenyerera kupulukira kwa anthu awa, kapena choipa chao, kapena tchimo lao; kuti linganene dziko limene mudatitulutsako, Popeza Yehova sanakhoze kuwalowetsa m'dziko limene adanena nao, ndi popeza anadana nao, anawatulutsa kuti awaphe m'chipululu. Koma iwo ndiwo anthu anu ndi cholowa chanu, amene mudatulutsa ndi mphamvu yanu yaikulu ndi dzanja lanu lotambasuka. Masiku aja Yehova anati kwa ine, Dzisemere magome awiri amiyala onga oyamba aja, nukwere kuno kwa Ine m'phiri umu, nudzipangire likasa lamtengo. Ndipo ndidzalembera pa magomewo mauwo anali pa magome oyamba aja amene unawaswa, ndipo uwaike m'likasamo. Potero ndinapanga likasa la mtengo wakasiya, ndinasemanso magome awiri amiyala onga oyamba aja, ndi kukwera m'phirimo, magome awiri ali m'manja mwanga. Ndipo analembera pamagome, monga mwa malembedwe oyamba, mau khumiwo, amene Yehova adanena ndi inu m'phirimo, ali pakati pa moto, tsiku la kusonkhanako; ndipo Yehova anandipatsa awa. Ndipo ndinatembenuka ndi kutsika m'phiri, ndi kuika magome m'likasa ndinalipanga, ali m'menemo monga Yehova anandilamulira ine. Ndipo ana a Israele anayenda ulendo wao kuchokera ku zitsime za ana a Yaakani kufikira ku Mosera. Kumeneko anamwalira Aroni, ndi kumeneko anamuika; ndipo Eleazara mwana wake anachita ntchito ya nsembe m'malo mwake. Kuchokerako ananka ulendo ku Gudigoda, ndi kuchokera ku Gudigoda kunka ku Yotibata, dziko la mitsinje yamadzi. Masiku aja Yehova anapatula fuko la Levi, linyamule likasa la chipangano la Yehova, liimirire pamaso pa Yehova kumtumikira, ndi kudalitsa m'dzina lake kufikira lero lino. Chifukwa chake Levi alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi abale ake; Yehova mwini wake ndiye cholowa chake, monga Yehova Mulungu wake ananena naye. Ndipo ndinakhala m'phiri monga poyamba paja, masiku makumi anai usana ndi usiku; ndipo Yehova anandimvera ine pameneponso; Yehova sanafune kukuonongani. Ndipo Yehova anati kwa ine, Uka, tenga ulendo pamaso pa anthu; kuti alowe ndi kulandira dzikoli ndinalumbirira makolo ao kuti ndidzawapatsa. Ndipo tsopano, Israele, Yehova Mulungu wanu afunanji nanu, koma kuti muziopa Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zake zonse, ndi kukonda, ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kusunga malamulo a Yehova, ndi malemba ake, amene ndikuuzani lero kuti kukukomereni inu? Taonani thambo, ndi kumwambamwamba, dziko lapansi, ndi zonse zili m'mwemo ndi zake za Yehova Mulungu wanu. Koma Yehova anakondwera nao makolo anu kuwakonda, nasankha mbeu zao zakuwatsata, ndiwo inu, mwa mitundu yonse ya anthu, monga kuli lero lino. Potero dulani khungu la mitima yanu, ndipo musamapulukiranso. Popeza Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wa milungu, ndi Mbuye wa ambuye; Mulungu wamkulu, wamphamvu, ndi woopsa, wosasamalira nkhope za anthu, kapena kulandira chokometsera mlandu. Aweruzira ana amasiye ndi mkazi wamasiye; ndipo akonda mlendo, ndi kumpatsa chakudya ndi chovala. M'mwemo mukondane naye mlendo; popeza munali alendo m'dziko la Ejipito. Muziopa Yehova Mulungu wanu; mumtumikire Iyeyo; mummamatire Iye, ndi kulumbira pa dzina lake. Iye ndiye lemekezo lanu, Iye ndiye Mulungu wanu, amene anachita nanu zazikulu ndi zoopsa izi, mudaziona m'maso mwanu. Makolo anu anatsikira ku Ejipito ndiwo anthu makumi asanu ndi awiri; ndipo Yehova Mulungu wanu anakusandulizani tsopano muchuluke ngati nyenyezi za kumwamba. Chifukwa chake muzikonda Yehova Mulungu wanu, ndi kusunga chilangizo chake, ndi malemba ake, ndi maweruzo ake, ndi malamulo ake, masiku onse. Ndipo dziwani lero lino; pakuti sindinena ndi ana anu osadziwa, ndi osapenya kulanga kwa Yehova Mulungu wanu, ukulu wake, dzanja lake lamphamvu, ndi mkono wake wotambasuka, ndi zizindikiro zake, ndi ntchito zake, adazichitira Farao mfumu ya Aejipito, ndi dziko lake lonse pakati pa Ejipito; ndi chochitira Iye nkhondo ya Ejipito, akavalo ao, ndi agaleta ao; kuti anawamiza m'madzi a Nyanja Yofiira, muja anakutsatani m'mbuyo, ndi kuti Yehova anawaononga kufikira lero lino; ndi chimene anakuchitirani m'chipululu, kufikira munadza kumalo kuno; ndi chimene anachitira Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu, mwana wa Rubeni; muja nthaka inatsegula pakamwa pake, ndi kuwameza iwo, ndi mabanja ao, ndi mahema ao, ndi za moyo zonse zakuwatsata pakati pa Israele wonse. Koma maso anu anapenya ntchito yonse yaikulu ya Yehova anaichita. Potero muzisunga malamulo onsewa ndikuuzani lero lino, kuti mukhale amphamvu, ndi kulowa ndi kulandira dziko, limene mumkako kulilandira; ndi kuti masiku anu achuluke m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, kuti adzawapatsa iwo ndi mbeu zao, dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi. Pakuti dziko limene mumkako kulilandira ndi losanga dziko la Ejipito lija mudatulukako, kumene kuja munafesa mbeu zanu, ndi kuzithirira ndi phazi lanu, monga munda watherere; koma dziko limene mumkako kulilandira ndilo dziko la mapiri ndi zigwa; limamwa madzi a mvula ya kumwamba; ndilo dziko loti Yehova Mulungu wanu alisamalira, maso a Yehova Mulungu wanu akhalapo chikhalire, kuyambira chaka mpaka kutsiriza chaka. Ndipo kudzakhala mukasamalira chisamalire malamulo anga amene ndikuuzani lero lino, kukonda Yehova Mulungu wanu, ndi kumtumikira ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndidzapatsa mvula ya dziko lanu m'nyengo yake, ya chizimalupsa ndi ya masika, kuti mutute tirigu wanu, ndi vinyo wanu, ndi mafuta anu. Ndipo ndidzapatsa msipu wa zoweta zanu podyetsa panu; mudzadyanso nimudzakhuta. Dzichenjerani nokha, angachete mitima yanu, nimungapatuke, ndi kutumikira milungu ina, ndi kuipembedza; ndi kuti Mulungu angapse mtima pa inu, nangatseke kumwamba, kuti isowe mvula, ndi kuti nthaka isapereke zipatso zake; ndi kuti mungaonongeke msanga m'dziko lokomali Yehova akupatsani. Chifukwa chake muzisunga mau anga awa mumtima mwanu ndi m'moyo mwanu; ndi kuwamanga ngati chizindikiro pamanja panu; ndipo zikhale zapamphumi pakati pa maso anu. Ndipo muziwaphunzitsa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala inu pansi m'nyumba mwanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pakuuka inu pomwe. Ndipo muziwalembera pa mphuthu za nyumba zanu, ndi pa zipata zanu; kuti masiku anu ndi masiku a ana anu achuluke m'dziko limene Yehova analumbira kwa makolo anu kuti adzawapatsali, monga masiku a thambo lili pamwamba pa dziko. Pakuti mukasunga chisungire malamulo awa onse amene ndikuuzani kuwachita; kukonda Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zake zonse, ndi kummamatira; Yehova adzapirikitsa amitundu awa onse pamaso panu, ndipo mudzalanda amitundu akulu ndi amphamvu oposa inu. Pamalo ponse padzapondapo phazi lanu ndi panu, kuyambira chipululu ndi Lebanoni, kuyambira pa mtsinjewo, mtsinje wa Yufurate, kufikira nyanja ya m'tsogolo, ndiwo malire anu. Palibe munthu adzaima pamaso panu; Yehova Mulungu wanu adzanjenjemeretsa ndi kuopsa dziko lonse mudzapondapo, chifukwa cha inu, monga anenana ndi inu. Taonani, ndilikuika pamaso panu lero dalitso ndi temberero; dalitso, ngati mudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikuuzani lero lino; koma temberero, ngati simudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi kupatuka m'njira ndikuuzani lero lino, kutsata milungu ina imene simunaidziwa. Ndipo kudzakhala, atakulowetsani Yehova Mulungu wanu m'dziko limene mumkako kulilandira, munene mdalitso pa phiri la Gerizimu, ndi temberero pa phiri la Ebala. Sakhala kodi tsidya lija la Yordani, m'tseri mwake mwa njira yake yolowa dzuwa, m'dziko la Akanani, akukhala m'chidikha, pandunji pake pa Giligala, pafupi pa mathundu a More? Pakuti mulinkuoloka Yordani kulowa ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani; ndipo mudzachilandira cholowa chanu, ndi kukhalamo. Potero samalirani kuchita malemba ndi maweruzo onse ndiwaika pamaso panu lero lino. Awa ndi malemba ndi maweruzo, muziwasamalirawa kuwachita m'dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu anakupatsani likhale lanulanu, masiku onse akukhala ndi moyo inu pa dziko lapansi. Muononge konse malo onse, amitundu amene mudzawalanda anatumikirako milungu yao, pa mapiri aatali, ndi pa zitunda, ndi pansi pa mitengo yonse yabiriwiri; nimugumule maguwa ao a nsembe, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kutentha zifanizo zao, ndi kulikha mafano osema a milungu yao; ndipo muononge dzina lao lichoke m'malomo. Musamatero ndi Yehova Mulungu wanu. Koma kumalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha mwa mafuko anu onse kuikapo dzina lake, ndiko ku chokhalamo chake, muzifunako, ndi kufikako; ndi kubwera nazo kumeneko nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zophera, ndi magawo anu onse a magawo khumi, ndi nsembe yokweza ya dzanja lanu, ndi zowinda zanu, ndi nsembe zanu zaufulu, ndi zoyamba kubadwa za ng'ombe zanu, ndi za nkhosa ndi mbuzi zanu; ndipo kumeneko muzidya pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kukondwera nazo zonse mudazigwira ndi dzanja lanu, inu ndi a pa banja lanu, m'mene Yehova Mulungu wanu anakudalitsani. Musamadzichita monga mwa zonse tizichita kuno lero, yense kuchita chilichonse chiyenera m'maso mwake; pakuti mpaka lero simunafikira mpumulo ndi cholowa, zimene Yehova Mulungu wanu adzakupatsani. Koma mudzaoloka Yordani, ndi kukhala m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akulandiritsani; ndipo adzakupumulitsani akulekeni adani anu onse pozungulirapo, ndipo mudzakhala mokhazikika. Pamenepo padzakhala malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake, kumeneko muzibwera nazo zonse ndikuuzanizi; nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zophera, magawo anu onse a magawo khumi, ndi nsembe yokweza dzanja lanu, ndi zowinda zanu zosankhika zimene muzilonjezera Yehova. Ndipo mudzakondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi ana anu amuna, ndi ana anu akazi, ndi antchito anu amuna, ndi antchito anu akazi, ndi Mlevi ali m'midzi mwanu, popeza alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi inu. Dzichenjerani nokha, musamapereka nsembe zanu zopsereza pamalo ponse upaona: koma pamalo pamene Yehova adzasankha, mwa limodzi la mafuko anu, pamenepo muzipereka nsembe zanu zopsereza, ndi pamenepo muzichita zonse ndikuuzani. Koma monga mwa chikhumbu chonse cha moyo wanu muiphe ndi kudya nyama m'midzi yanu yonse, monga mwa mdalitso wa Yehova Mulungu wanu anakupatsani; odetsa ndi oyera adyeko, monga yamphoyo ndi yangondo. Mwazi wao wokha musamadya; muziuthira panthaka ngati madzi. Simukhoza kudya m'mudzi mwanu limodzi la magawo khumi la tirigu wanu, kapena la vinyo wanu, kapena la mafuta anu, kapena oyamba kubadwa a ng'ombe zanu kapena la nkhosa ndi mbuzi zanu, kapena zowinda zanu zilizonse muzilonjeza kapena nsembe zanu zaufulu, kapena nsembe yokweza ya m'dzanja lanu; koma muzizidya pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha, inu, ndi ana anu amuna, ndi ana anu akazi, ndi antchito anu amuna, ndi antchito anu akazi, ndi Mlevi ali m'mudzi mwanu; nimukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'zonse mudazigwira ndi dzanja lanu. Dzichenjerani nokha, musataye Mlevi masiku onse akukhala inu m'dziko mwanu. Akadzakuza malire a dziko lanu Yehova Mulungu wanu, monga ananena ndi inu, ndipo mukadzati, Ndidye nyama, popeza moyo wanga ukhumba kudya nyama; mudye nyama monga umo monse ukhumba moyo wanu. Malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kuikako dzina lake akakutanimphirani, muziphako ng'ombe zanu ndi nkhosa ndi mbuzi zanu zimene Yehova anakupatsani, monga ndinakuuzani, ndi kuzidya m'mudzi mwanu, monga umo monse ukhumba moyo wanu. Koma monga umo amadya mphoyo ndi ngondo momwemo uzizidya; odetsa ndi oyera adyeko chimodzimodzi. Koma mulimbikepo ndi kusadya mwaziwo; popeza mwazi ndiwo moyo, nimusamadya moyo pamodzi ndi nyama yake. Musamadya uwu; muuthire pansi ngati madzi. Musamadya uwu; kuti chikukomereni inu, ndi ana anu akudza m'mbuyo mwanu, pakuchita inu zoyenera pamaso pa Yehova. Zopatulika zanu zokha zimene muli nazo, ndi zowinda zanu, muzitenge, ndi kupita nazo ku malo amene Yehova adzasankha; ndipo mupereke nsembe zanu zopsereza, nyama zao ndi mwazi wao, pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu; ndipo athire mwazi wa nsembe zanu zophera pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu, koma nyama yake muidye. Samalirani ndi kumvera mau awa onse ndikuuzaniwa, kuti chikukomereni inu, ndi ana anu akudza m'mbuyo mwanu nthawi zonse, pochita inu zokoma ndi zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wanu. Pamene Yehova Mulungu wanu akadzadulatu amitundu pamaso panu, kumene mulowako kuwalandira, ndipo mutawalandira, ndi kukhala m'dziko lao, dzichenjerani nokha mungakodwe ndi kuwatsata, ataonongeka pamaso panu; ndi kuti mungafunsire milungu yao, ndi kuti, Amitundu awa atumikira milungu yao bwanji? Ndichite momwemo inenso. Musamatero ndi Yehova Mulungu wanu; pakuti zilizonse zinyansira Yehova, zimene azida Iye, iwowa anazichitira milungu yao; pakuti angakhale ana ao amuna ndi ana ao akazi awatentha m'moto, nsembe ya milungu yao. Chilichonse ndikuuzani, muchisamalire kuchichita; musamaonjezako, kapena kuchepsako. Akauka pakati pa inu mneneri, kapena wakulota maloto, nakakupatsani chizindikiro kapena chozizwa; ndipo chizindikiro kapena chozizwa adanenachi chifika, ndi kuti, Titsate milungu ina, imene simunaidziwa, ndi kuitumikira; musamamvera mau a mneneri uyu, kapena wolota maloto uyu; popeza Yehova Mulungu wanu akuyesani, kuti adziwe ngati mukonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse. Muziyenda kutsata Yehova Mulungu wanu, ndi kumuopa, ndi kusunga malamulo ake, ndi kumvera mau ake, ndi kumtumikira Iye, ndi kummamatira. Ndipo mneneriyo, kapena wolota malotoyo, mumuphe; popeza ananena chosiyanitsa ndi Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani m'dziko la Ejipito, nakuombolani m'nyumba ya akapolo; kuti akucheteni mutaye njira imene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani muziyendamo. Potero muzichotsa choipacho pakati pa inu. Mbale wanu, ndiye mwana wa mai wanu, kapena mwana wanu wamwamuna, kapena mwana wanu wamkazi, kapena mkazi wa kumtima kwanu, kapena bwenzi lanu, ndiye ngati moyo wanuwanu, akakukakamizani m'tseri, ndi kuti, Tipite titumikire milungu ina, imene simunaidziwa, inu, kapena makolo anu; ndiyo milungu ya mitundu ya anthu akuzungulira inu, akukhala pafupi pali inu, kapena akukhala patali pali inu, kuyambira malekezero a dziko lapansi kufikira malekezero ena a dziko lapansi; musamavomerezana naye, kapena kumvera iye; diso lanu lisamchitire chifundo, kapena kumleka, kapena kumbisa; koma muzimupha ndithu; liyambe dzanja lanu kukhala pa iye kumupha, ndi pamenepo dzanja la anthu onse. Nimuzimponya miyala, kuti afe; popeza anayesa kukuchetani muleke Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani m'dziko la Ejipito, m'nyumba ya akapolo. Kuti Israele wonse amve, ndi kuopa, ndi kusaonjeza kuchita choipa chotere chonga ichi pakati pa inu. Ukamva za umodzi wa midzi yanu, imene Yehova Mulungu wanu akupatsani kukhalako, ndi kuti, Amuna ena opanda pake anatuluka pakati pa inu, nacheta okhala m'mudzi mwao, ndi kuti, Timuke titumikire milungu ina, imene simunaidziwa; pamenepo muzifunsira, ndi kulondola, ndi kufunsitsa; ndipo taonani, chikakhala choona, chatsimikizika chinthuchi, kuti chonyansa chotere chachitika pakati pa inu; muzikanthatu okhala m'mudzi muja ndi lupanga lakuthwa; ndi kuononga konse, ndi zonse zili m'mwemo, ng'ombe zake zomwe, ndi lupanga lakuthwa. Ndipo muzikundika zofunkha zake zonse pakati pakhwalala pake, nimutenthe ndi moto mudzi, ndi zofunkha zake zonse konse, pamaso pa Yehova Mulungu wanu; ndipo udzakhala mulu ku nthawi zonse; asaumangenso. Ndipo pasamamatire padzanja panu kanthu ka chinthu choti chionongeke; kuti Yehova aleke mkwiyo wake waukali, nakuchitireni chifundo, ndi kukumverani nsoni, ndi kukuchulukitsani monga analumbirira makolo anu; pakumvera inu mau a Yehova Mulungu wanu, kusunga malamulo ake onse amene ndikuuzani lero lino, kuchita zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wanu. Inu ndinu ana a Yehova Mulungu wanu; musamadzicheka, kapena kumeta tsitsi pakati pa maso chifukwa cha akufa. Popeza ndinu mtundu wa anthu opatulikira Yehova Mulungu wanu, ndipo Yehova anakusankhani mukhale mtundu wa anthu wa pa wokha wa Iye yekha, mwa mitundu yonse ya anthu okhala pankhope pa dziko lapansi. Musamadya chonyansa chilichonse. Nyamazi muyenera kumadya ndi izi: ng'ombe, nkhosa, ndi mbuzi, ngondo, ndi nswala ndi mphoyo, ndi mphalapala, ndi ngoma, ndi nyumbu, ndi mbalale. Ndipo nyama iliyonse yogawanika chiboda, nikhala yogawanikadi chiboda, nibzikula, imeneyo muyenera kudya. Koma izi zokha simuyenera kuzidya mwa zobzikulazo, kapena zogawanika chiboda: ngamira, ndi kalulu, ndi mbira, popeza zibzikula, koma zosagawanika chiboda, muziyese zodetsa; ndi nkhumba, popeza igawanika chiboda koma yosabzikula, muiyese yodetsa; musamadya nyama yao, musamakhudza mitembo yao. Mwa zonse zili m'madzi muyenera kumadya izi: zilizonse zili nazo zipsepse ndi mamba, zimenezi muyenera kumadya; koma zilizonse zopanda zipsepse kapena mamba musamadya; muziyese zonyansa. Mbalame zosadetsa zonse muyenera kumadya. Koma izi ndi zimene simuyenera kumadya: mphungu, ndi nkhwazi, ndi chikambi, ndi kamtema, ndi mphamba, ndi muimba monga mwa mtundu wake; ndi khungubwi aliyense monga mwa mtundu wake; ndi nthiwatiwa, ndi chipudo, ndi kakowa, ndi kabawi monga mwa mtundu wake; ndi nkhutukutu, ndi manchichi, ndi tsekwe; ndi vuwo, ndi dembo, ndi nswankhono; ndi indwa, ndi chimeza, monga mwa mtundu wake, ndi sadzu, ndi mleme. Ndipo zokwawa zonse zakuuluka muziyesa zonyansa; musamazidya. Mbalame zonse zosadetsa muyenera kumadya. Musamadya chinthu chilichonse chitafa chokha; muzipereka icho kwa mlendo ali m'mudzi mwanu, achidye ndiye; kapena uchigulitse kwa mlendo; popeza ndinu mtundu wa anthu wopatulika wa Yehova Mulungu wanu. Musamaphika mwanawambuzi mu mkaka wa make. Muzipereka ndithu limodzi la magawo khumi la zipatso zonse za mbeu zanu, zofuma kumunda, chaka ndi chaka. Ndipo muzidye pamaso pa Yehova Mulungu wanu, m'malo m'mene asankhamo Iye, kukhalitsamo dzina lake; limodzi la magawo khumi la tirigu wanu, la vinyo wanu, ndi la mafuta anu, ndi oyamba kubadwa a ng'ombe zanu ndi a nkhosa ndi mbuzi zanu; kuti muphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu masiku onse. Ndipo ikakutalikirani njira kotero kuti simukhoza kulinyamula, popeza malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha, kuikapo dzina lake, akutanimphirani; atakudalitsani Yehova Mulungu wanu; pamenepo mulisinthe ndalama, ndi kumanga ndalama ikhale m'dzanja mwanu, ndi kupita ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha; ndipo mugule ndi ndalamazo chilichonse moyo wanu ukhumba, ng'ombe kapena nkhosa, kapena vinyo, kapena chakumwa cholimba, kapena chilichonse moyo wanu ukufunsani; nimudye pomwepo pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kukondwera, inu ndi a pabanja panu. Koma Mlevi wokhala m'mudzi mwanu, musamamtaya, popeza alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi inu. Pakutha pake pa zaka zitatu muzitulutsa magawo onse a magawo khumi a zipatso zanu za chaka icho, ndi kuwalinditsa m'mudzi mwanu; ndipo abwere Mlevi, popeza alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi inu, ndi mlendo, ndi ana amasiye, ndi mkazi wamasiye, okhala m'mudzi mwanu, nadye nakhute; kuti Yehova Mulungu wanu akakudalitseni mu ntchito zonse za dzanja lanu muzichitazi. Pakutha pake pa zaka zisanu ndi ziwiri pakhale chilekerero. Chilekererocho ndichi: okongoletsa onse alekerere chokongoletsa mnansi wake; asachifunse kwa mnansi wake, kapena mbale wake; popeza analalikira chilekerero cha Yehova. Muyenera kuchifunsa kwa mlendo; koma chanu chilichonse chili ndi mbale wanu, dzanja lanu lichilekerere; ndiko kuti pasakhale waumphawi mwa inu; pakuti Yehova adzakudalitsani kwambiri m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanuchanu; chokhachi mumvere chimverere mau a Yehova Mulungu wanu, kuti musamalire kuchita malamulo awa onse amene ndikuuzani lero lino. Popeza Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani, monga ananena nanu; ndipo mudzakongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha; nimudzachita ufumu pa amitundu ambiri, koma iwo sadzachita ufumu pa inu. Akakhala ndi inu munthu waumphawi, ndiye wina wa abale anu, m'umodzi wa midzi yanu, m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, musakhakala mtima wanu, kapena kuumitsa dzanja lanu kukaniza mbale wanu waumphawi; koma muzimtansira dzanja lanu ndithu ndi kumkongoletsa ndithu zofikira kusowa kwake, monga umo amasowa. Dzichenjerani, mungakhale mau opanda pake mumtima mwanu, ndi kuti, Chayandika chaka chachisanu ndi chiwiri, chaka cha chilekerero; ndipo diso lanu lingaipire mbale wanu waumphawi, osampatsa kanthu; ndipo iye angalirire inu kwa Yehova; ndipo mwa inu mungakhale tchimo. Muzimpatsa ndithu, osawawa mtima wanu pompatsa; popeza, chifukwa cha ichi Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mu ntchito zanu zonse, ndi m'zonse muikapo dzanja lanu. Popeza waumphawi salekana m'dziko, chifukwa chake ndikuuzani ndi kuti, Dzanja lanu mulitansire ndithu mbale wanu, ndi ozunzika anu, ndi aumphawi anu, a m'dziko mwanu. Mukagula mbale wanu, Muhebri wamwamuna kapena Muhebri wamkazi, ndipo adzakutumikira zaka zisanu ndi chimodzi; koma chaka chachisanu ndi chiwiri umlole achoke kwanu waufulu. Ndipo pomlola iwe achoke kwanu waufulu, musamamlola achoke wopanda kanthu; mumlemeze nazo za nkhosa ndi mbuzi zanu, ndi za popondera mphesa, ndi za mosungira vinyo; monga Yehova Mulungu wanu anakudalitsani mumninkhe uyu. Ndipo mukumbukire kuti munali akapolo m'dziko la Ejipito, ndipo Yehova Mulungu wanu anakuombolani; chifukwa chake ndikuuzani ichi lero lino. Ndipo kudzakhala, akanena ndi inu, Sindituluka kuchoka kwanu; popeza akonda inu ndi nyumba yanu, popeza kumkomera kwanu; pamenepo muzitenga lisungulo, ndi kulipisa m'khutu mwake, kulikanikiza ndi chitseko, ndipo adzakhala kapolo wanu kosalekeza. Muzichitanso momwemo ndi adzakazi anu. Musamayesa nchosautsa, pomlola akuchokereni waufulu; popeza anakugwirirani ntchito zaka zisanu ndi chimodzi monga wolipidwa wakulandira chowirikiza; potero Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani m'zonse muzichita. Zazimuna zonse zoyamba kubadwa, zobadwa mwa ng'ombe zanu ndi mwa nkhosa ndi mbuzi zanu, muzizipatulira Yehova Mulungu wanu; musamagwiritsa ntchito yoyamba kubadwa mwa ng'ombe zanu, kapena kusenga yoyamba kubadwa ya nkhosa kapena mbuzi zanu. Muzidye chaka ndi chaka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, m'malo amene Yehova adzasankha, inu ndi a m'banja mwanu. Koma ikakhala nacho chilema, yotsimphina, kapena yakhungu, chilema chilichonse choipa, musamaiphera nsembe Yehova Mulungu wanu. Muidye m'mudzi mwanu; odetsa ndi oyera aidye chimodzimodzi, monga mphoyo ndi nswala. Mwazi wake wokha musamadya; muuthire pansi ngati madzi. Samalirani mwezi wa Abibu, kuti muzichitira Yehova Mulungu wanu Paska; popeza m'mwezi wa Abibu Yehova Mulungu wanu anakutulutsani m'dziko la Ejipito usiku. Ndipo muziphera Yehova Mulungu wanu nsembe ya Paska, ya nkhosa ndi ya ng'ombe, m'malo amene Yehova adzasankha kukhalitsamo dzina lake. Musamadyera nayo mkate wa chotupitsa; masiku asanu ndi awiri mudyere nayo mkate wopanda chotupitsa, ndiwo mkate wa chizunziko popeza munatuluka m'dziko la Ejipito mofulumira; kuti mukumbukire tsiku lotuluka inu m'dziko la Ejipito masiku onse a moyo wanu. Ndipo m'malire mwanu monse musaoneke chotupitsa masiku asanu ndi awiri; nyama yomwe muiphere nsembe tsiku loyamba madzulo, isatsaleko usiku wonse kufikira m'mawa. Simuyenera kuphera nsembe ya Paska m'midzi yanu iliyonse, imene Yehova Mulungu wanu akupatsani; koma pamalo pamene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsapo dzina lake, pamenepo muphere nsembe ya Paska, madzulo, polowa dzuwa, nyengo ya kutuluka inu m'Ejipito. Ndipo muiphike ndi kuidya m'malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha; koma m'mawa mwake mubwerere kunka ku mahema anu. Masiku asanu ndi limodzi muzidya mkate wopanda chotupitsa; ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo loletsa, la Yehova Mulungu wanu; musamagwira ntchito pamenepo. Mudziwerengere masabata asanu ndi awiri; muyambe kuwerenga masabata asanu ndi awiri poyambira kusenga tirigu wachilili. Ndipo muchitire Yehova Mulungu wanu chikondwerero cha Masabata, ndiwo msonkho waufulu wa dzanja lanu, umene mupereke monga Yehova Mulungu wanu akudalitsani. Ndipo mukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi ana anu amuna, ndi ana anu akazi, ndi antchito anu amuna, ndi antchito anu akazi, ndi Mlevi wokhala m'mudzi mwanu, ndi mlendo, ndi mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye, okhala pakati pa inu, m'malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake. Ndipo mukumbukire kuti munali akapolo m'Ejipito; musamalire kuchita malemba awa. Mudzichitire chikondwerero cha Misasa masiku asanu ndi awiri, mutasunga za padwale ndi za mopondera mphesa; nimukondwere m'madyerero mwanu, inu, ndi ana anu amuna, ndi ana anu akazi, ndi antchito anu amuna, ndi antchito anu akazi, ndi Mlevi, ndi mlendo, ndi mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye okhala m'mudzi mwanu. Masiku asanu ndi awiri muchitire Yehova Mulungu wanu madyerero m'malo amene Yehova adzasankha; popeza Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani m'zipatso zanu zonse, ndi m'ntchito zonse za manja anu; nimukondwere monsemo. Amuna onse azioneka pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'malo amene Iye adzasankha, katatu m'chaka; pa chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa, pa chikondwerero cha masabata, ndi pa chikondwerero cha Misasa; ndipo asaoneke pamaso pa Yehova opanda kanthu; apereke yense monga mwa mphatso ya m'dzanja lake, monga mwa mdalitso wa Yehova Mulungu wanu anakupatsani. Mudziikire oweruza ndi akapitao m'midzi yanu yonse imene Yehova Mulungu wanu akupatsani, monga mwa mafuko anu; ndipo aweruze anthu ndi chiweruzo cholungama. Musamapotoza chiweruzo, musamasamalira munthu, kapena kulandira chokometsera mlandu; popeza chokometsera mlandu chidetsa maso a anzeru, nichiipsa mau a olungama. Chilungamo, chilungamo ndicho muzichitsata, kuti mukhale ndi moyo ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani. Musazike zifanizo zilizonse pafupi pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu, limene mwadzimangira. Ndipo musamadziutsira choimiritsa chilichonse chimene Yehova Mulungu wanu adana nacho. Musamaphera Yehova Mulungu wanu nsembe ya ng'ombe, kapena nkhosa, yokhala nacho chilema, kapena chilichonse choipa; pakuti chinyansira Yehova Mulungu wanu. Akapeza pakati panu, m'mudzi wanu wina umene anakupatsani Yehova Mulungu wanu, wamwamuna kapena wamkazi wakuchita chili choipa pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kulakwira chipangano chake, nakatumikira milungu ina, naigwadira iyo, kapena dzuwa, kapena mwezi, kapena wina wa khamu la kuthambo, losauza Ine; ndipo akakuuzani, nimudamva, pamenepo muzifunsira, ndipo taonani, chikakhala choonadi, choti nzenizeni, chonyansachi chachitika m'Israele; pamenepo mutulutse mwamunayo kapena mkaziyo, anachita choipacho, kunka naye ku zipata zanu, ndiye wamwamuna kapena wamkazi; ndipo muwaponye miyala, kuti afe. Pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu amuphe iye amene akuti afe; asamuphe pakamwa pa mboni imodzi. Liyambe kumgwera dzanja la mboniyo kumupha; pamenepo dzanja la anthu onse. Potero muzichotsa choipacho pakati panu. Ukakukanikani mlandu pouweruza, ndiwo wakunena zamwazi, kapena zakutsutsana, kapena zakupandana, ndiyo milandu yakutengana m'midzi mwanu; pamenepo muziuka ndi kukwera kunka ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha; nimufike kwa ansembe, Alevi, ndi kwa woweruza wa m'masiku awo; nimufunsire; ndipo adzakufotokozerani maweruzidwe ake. Ndipo muchite monga momwe ananena mau akufotokozeraniwo, ku malo amene Yehova adzawasankha; nimusamalire kuchita monga mwa zonse akulangizanizi. Monga momwe anena malamulo akulangizani, ndi monga mwa chiweruzo akufotokozerani muchite; mau akufotokozerani musawapatukire kulamanja kapena kulamanzere. Koma munthu wakuchita modzikuza, osamvera wansembe wokhala chilili kutumikirako pamaso pa Yehova Mulungu wanu, kapena woweruza, munthuyo afe; ndipo muchotse choipacho kwa Israele. Ndipo anthu onse adzamva ndi kuchita mantha, osachitanso modzikuza. Mutakalowa m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, ndi kulilandira lanulanu, ndi kukhalamo; ndipo mukanena, Tidziikire mfumu, monga amitundu onse akutizinga; mumuiketu mfumu yanu imene Yehova Mulungu wanu adzaisankha; wina pakati pa abale anu mumuike mfumu yanu; simuyenera kudziikira mlendo, wosakhala mbale wanu. Koma asadzichulukitsire akavalo iye, kapena kubwereretsa anthu anke ku Ejipito, kuti achulukitse akavalo; popeza Yehova anati nanu, Musamabwereranso njira iyi. Ndipo asadzichulukitsire akazi, kuti ungapatuke mtima wake; kapena asadzichulukitsire kwambiri siliva ndi golide. Ndipo kudzali, pakukhala iye pa mpando wachifumu wa ufumu wake, adzilemberere chofanana cha chilamulo ichi m'buku, achitenge pa ichi chili pamaso pa ansembe Alevi; ndipo azikhala nacho, nawerengemo masiku onse a moyo wake; kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wake, kusunga mau onse a chilamulo ichi ndi malemba awa, kuwachita; kuti mtima wake usadzikuze pa abale ake, ndi kuti asapatukire lamulolo, kulamanja kapena kulamanzere; kuti achuluke masiku ake, m'ufumu wake, iye ndi ana ake pakati pa Israele. Ansembe Alevi, fuko lonse la Levi, alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi Israele; azizidya nsembe zamoto za Yehova, ndi cholowa chake. Alibe cholowa pakati pa abale ao; Yehova mwini wake ndiye cholowa chao, monga ananena nao. Ndipo zoyenera ansembe, awapatse anthu akuphera nsembe ndizo: ingakhale ng'ombe kapena nkhosa azipatsa wansembe mwendo wamwamba, ndi ya m'masaya ndi chifu. Zipatso zoyamba za tirigu wanu, za vinyo wanu, ndi za mafuta anu ndi ubweya woyamba kuusenga, muwapatse izi. Popeza Yehova Mulungu wanu anawasankha mwa mafuko anu onse, aimirire natumikire m'dzina la Yehova, iwo ndi ana ao amuna kosalekeza. Ndipo Mlevi akachokera kumudzi wanu wina m'Israele monse, kumene akhalako, nakadza ndi chifuniro chonse cha moyo wake ku malo amene Yehova adzasankha; pamenepo azitumikira m'dzina la Yehova Mulungu wake, monga amachita abale ake onse Alevi akuimirirako pamaso pa Yehova. Chakudya chao chizifanana, osawerengapo zolowa zake zogulitsa. Mutakalowa m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, musamaphunzira kuchita monga mwa zonyansa za amitundu aja. Asapezeke mwa inu munthu wakupitiriza mwana wake wamwamuna kapena mwana wake wamkazi ku moto wa ula, wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga. Kapena wotsirika, kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa. Popeza aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye; ndipo chifukwa cha zonyansa izi Yehova Mulungu wanu awapirikitsa pamaso panu. Mukhale angwiro ndi Yehova Mulungu wanu. Pakuti amitundu awa amene mudzawalandira, amamvera iwo akuyesa mitambo, ndi a ula; koma inu, Yehova Mulungu wanu sakulolani kuchita chotero. Yehova Mulungu wanu adzakuukitsirani mneneri wa pakati panu, wa abale anu, wonga ine; muzimvera iye; monga mwa zonse munafunsa Yehova Mulungu wanu m'Horebu, tsiku lakusonkhana lija, ndi kuti, Tisamvenso mau a Yehova Mulungu wathu, ndipo tisaonenso moto waukulu uwu, kuti tingafe. Ndipo Yehova anati kwa ine, Chokoma ananenachi. Ndidzawaukitsira mneneri wa pakati pa abale ao, wonga iwe; ndipo ndidzampatsa mau anga m'kamwa mwake, ndipo adzanena nao zonse ndimuuzazi. Ndipo kudzakhala kuti munthu wosamvera mau anga amene amanena m'dzina langa, ndidzamfunsa. Koma mneneri wakuchita modzikuza ndi kunena mau m'dzina langa, amene sindinamlamulira anene, kapena kunena m'dzina la milungu ina, mneneri ameneyo afe. Ndipo mukati m'mtima mwanu, Tidzazindikira bwanji mau amene Yehova sananene? Mneneri akanena m'dzina la Yehova, koma mau adanenawa sachitika, nisafika, ndiwo mau Yehova sanawanene; mneneriyo ananena modzikuza, musamuope iye. Pamene Yehova Mulungu wanu ataononga amitundu, amene Yehova Mulungu wanu akupatsani dziko lao, ndipo mutalilandira lanulanu, ndi kukhala m'midzi mwao, ndi m'nyumba zao; pamenepo mudzipatulire midzi itatu pakati pa dziko lanu, limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanulanu. Mudzikonzere njira, ndi kugawa malire a dziko lanu, limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanulanu, patatu; kuti wakupha munthu athawireko. Ndipo mlandu wa munthu wakupha mnzake wakuthawirako nakhala ndi moyo ndiwo: wakupha mnzake osati dala, osamuda kale lonse; monga ngati munthu analowa kunkhalango ndi mnzake kutema mitengo, ndi dzanja lake liyendetsa nkhwangwa kutema mtengo, ndi nkhwangwa iguluka m'mpinimo, nikomana ndi mnzake, nafa nayo; athawire ku wina wa midzi iyi, kuti akhale ndi moyo; kuti wolipsa mwazi angalondole wakupha mnzake, pokhala mtima wake watentha, nampeza, popeza njira njaitali, namkantha kuti wafa; angakhale sanapalamule imfa, poona sanamude kale lonse. Chifukwa chake ndikuuzani ndi kuti, Mudzipatulire midzi itatu. Ndipo Yehova Mulungu wanu akakulitsa malire anu, monga analumbirira makolo anu, ndi kukupatsani dziko lonse limene ananena kwa makolo anu kuwapatsa ili; ukadzasunga lamulo ili lonse kulichita, limene ndikuuzani lero lino, kukonda Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m'njira zake masiku onse; pamenepo mudzionjezere midzi itatu ina pamodzi ndi itatu iyi; kuti angakhetse mwazi wosachimwa pakati pa dziko lanu, limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanu, pangakhale mwazi pa inu. Koma munthu akamuda mnzake, namlalira, ndi kumuukira ndi kumkantha moyo wake, kuti wafa; nakathawira ku wina wa midzi iyi; pamenepo akulu a mudzi wake atumize ndi kumtengako ndi kumpereka m'manja mwa wolipsa mwazi, kuti afe. Diso lanu lisamchitire chifundo, koma muchotse mwazi wosachimwa m'Israele, kuti chikukomereni. Musamasendeza malire a mnansi wanu, amene adawaika iwo a kale lomwe, m'cholowa chanu mudzalandirachi, m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanulanu. Mboni imodzi isamaukira munthu pa mphulupulu iliyonse, kapena tchimo lililonse adalichimwa; pakamwa pa mboni ziwiri, kapena pakamwa pa mboni zitatu mlandu utsimikizike. Mboni yachiwawa ikaukira munthu kumneneza ndi kuti analakwa; pamenepo anthu onse awiri, pakati pao pali makaniwo, aziima pamaso pa Yehova, pamaso pa ansembe ndi oweruza okhala m'masiku awa; ndipo oweruza afunsitse bwino; ndipo taonani, mboniyo ikakhala mboni yonama, yomnamizira mbale wake; mumchitire monga iye anayesa kumchitira mbale wake; motero muchotse choipacho pakati panu. Ndipo otsalawo adzamva, nadzaopa, ndi kusachitanso monga choipacho pakati panu. Ndipo diso lanu lisachite chifundo, moyo kulipa moyo, diso kulipa diso, dzino kulipa dzino, dzanja kulipa dzanja, phazi kulipa phazi. Pamene mutuluka pa mdani wanu kunkhondo, ndi kuona akavalo ndi magaleta ndi anthu akuchulukira inu, musawaopa; popeza Yehova Mulungu wanu, amene anakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito, ali ndi inu. Ndipo kudzali, pamene muyandikiza kunkhondo, ayandikize wansembe nanene ndi anthu, nati nao, Tamverani, Israele, muyandikiza kunkhondo lero pa adani anu; musafumuka mitima yanu; musachita mantha, kapena kunjenjemera, kapena kuopsedwa pamaso pao; pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye wakumuka nanu, kugwirira inu pa adani anu, kukupulumutsani. Ndipo akapitao anene ndi anthu, ndi kuti, Ndani munthuyo anamanga nyumba yatsopano, osalowamo? Amuke nabwerere kunyumba kwake, kuti angafe kunkhondo nangalowemo munthu wina. Ndipo ndani munthuyo anaoka munda wamphesa osalawa zipatso zake? Amuke nabwerere kunyumba yake, kuti angafe kunkhondo, nangalawe munthu wina zipatso zake. Ndipo munthuyo ndani anapala bwenzi ndi mkazi osamtenga? Amuke nabwerere kunyumba kwake, kuti angafe kunkhondo, nangamtenge munthu wina. Pamenepo akapitao anenenso kwa anthu, ndi kuti, Munthuyo ndani wakuchita mantha ndi wofumuka mtima? Amuke nabwerere kunyumba kwake, ingasungunuke mitima ya abale ake monga mtima wake. Ndipo kudzali, atatha akapitao kunena ndi anthu, aike akazembe a makamu atsogolere anthu. Pamene muyandikiza mudzi kuchita nao nkhondo, muziufuulira ndi mtendere. Ndipo kudzali, ukakubwezerani mau a mtendere, ndi kukutsegulirani, pamenepo anthu onse opereka m'mwemo akhale akapolo anu, nadzakugwirirani ntchito yathangata. Koma ukapanda kuchita zamtendere ndi inu, koma kuchita nkhondo nanu, pamenepo muumangire tsasa. Ndipo pamene Yehova Mulungu wanu aupereka m'dzanja lanu, mukanthe amuna ake onse ndi lupanga lakuthwa. Koma akazi ndi ana ndi ng'ombe ndi zonse zili m'mudzimo, zankhondo zake zonse, mudzifunkhire nokha; ndipo mudye zankhondo za adani anu, zimene Yehova Mulungu wanu anakupatsani. Muzitero nayo midzi yonse yokhala kutalitali ndi inu, yosakhala midzi ya amitundu awa. Koma za midzi ya amitundu awa, imene Yehova Mulungu wanu akupatsani, ikhale cholowa chanu, musasiyepo chamoyo chilichonse chakupuma; koma muwaononge konse Ahiti, ndi Aamori, Akanani, ndi Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi; monga Yehova Mulungu wanu anakulamulirani; kuti angakuphunzitseni kuchita monga mwa zonyansa zao zonse, amazichitira milungu yao; ndipo mungachimwire Yehova Mulungu wanu. Pamene mumangira tsasa mudzi masiku ambiri, pouthirira nkhondo kuugwira, usamaononga mitengo yake ndi kuitema ndi nkhwangwa; pakuti ukadyeko, osailikha; pakuti mtengo wa m'munda ndiwo munthu kodi kuti uumangire tsasa? Koma mitengo yoidziwa inu kuti si ndiyo mitengo yazipatso, imeneyi muiononge ndi kuilikha; ndipo mudzi wochita nanu nkhondo muumangire machemba, mpaka mukaugonjetsa. Akapeza munthu waphedwa m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanulanu, nagona pamunda, wosadziwika wakumkantha, pamenepo azituluka akulu anu ndi oweruza anu, nayese kumidzi yomzinga wophedwayo; ndipo kudzali kuti mudzi wakukhala kufupi kwa munthu wophedwayo, inde akulu a mudzi uwu atenge ng'ombe yaikazi yosagwira ntchito, yosakoka goli; ndipo akulu a mudzi uwu atsike nayo ng'ombeyo ku chigwa choyendako madzi, chosalima ndi chosabzala, nayidula khosi ng'ombeyo m'chigwamo; ndipo ansembe, ana a Levi, ayandikize; pakuti Yehova Mulungu wanu anasankha iwo kumtumikira ndi kudalitsa m'dzina la Yehova; ndipo kutengana konse ndi kupandana konse kukonzeke monga mwa mau awa. Ndipo akulu onse a mudziwo wokhala pafupi pa munthu wophedwayo azisamba manja ao pa ng'ombeyo yodulidwa khosi m'chigwamo; nayankhe nati, Manja athu sanakhetse mwazi uwu, ndi maso athu sanauone. Landirani, Yehova, chotetezera anthu anu Israele, amene munawaombola, ndipo musalole mwazi wosachimwa ukhale pakati pa anthu anu Israele; ndipo adzawatetezera cha mwaziwo. Chotero mudzichotsere mwazi wosachimwa pakati panu, pakuti wachita choyenera pamaso pa Yehova. Pamene mutuluka kunka ku nkhondo ya pa adani anu, ndipo Yehova Mulungu wanu awapereka m'manja mwanu, ndipo muwagwira akhale akapolo anu; mukaona mwa akapolowa mkazi wokongola, mukamkhumba, ndi kufuna mumtenga akhale mkazi wanu; pamenepo mufike naye kwanu kunyumba yanu; ndipo amete tsitsi la pamutu pake, ndi kutenga makadabo ake; navule zovala za ukapolo wake, nakhale m'nyumba mwanu, nalire atate wake, ndi mai wake mwezi wamphumphu; ndipo atatero mulowe naye ndi kukhala mwamuna wake, ndi iye akhale mkazi wanu. Ndipo kudzali, mukapanda kukondwera naye, mumlole apite komwe afuna; koma musamgulitsa ndalama konse, musamamuyesa chuma, popeza wamchepetsa. Munthu akakhala nao akazi awiri, wina wokondana naye, wina wodana naye, nakambalira ana, wokondana naye, ndi wodana naye yemwe; ndipo mwana wamwamuna woyamba akakhala wa iye uja anadana naye; pamenepo kudzali, tsiku lakugawira ana ake amuna chuma chake, sangakhoze kuyesa mwana wa wokondana naye woyamba kubadwa, wosati mwana wa wodana naye, ndiye woyamba kubadwatu. Koma azivomereza wobadwa woyamba, mwana wa wodana naye, ndi kumwirikizira gawo lake la zake zonse; popeza iye ndiye chiyambi cha mphamvu yake; zoyenera woyamba kubadwa nzake. Munthu akakhala naye mwana wamwamuna wopulukira, ndi wopikisana naye, wosamvera mau a atate wake, kapena mau a mai wake, wosawamvera angakhale anamlanga; azimgwira atate wake ndi mai wake, ndi kutulukira naye kwa akulu a mudzi wake, ndi ku chipata cha malo ake; ndipo anene kwa akulu a mudzi wake, Mwana wathu wamwamuna uyu ngwopulukira ndi wopikisana nafe, wosamvera mau athu, ndiye womwazamwaza, ndi woledzera. Pamenepo amuna onse a mudzi wake amponye miyala kuti afe; chotero muchotse choipacho pakati panu; ndipo Israele wonse adzamva, nadzaopa. Munthu akakhala nalo tchimo loyenera imfa, kuti amuphe, ndipo wampachika; mtembo wake usakhale pamtengo usiku wonse, koma mumuike ndithu tsiku lomwelo; pakuti wopachikidwa pamtengo atembereredwa ndi Mulungu; kuti mungadetse dziko lanu limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanu. Mukapenya ng'ombe kapena nkhosa ya mbale wako zilikusokera musamazilekerera, muzimbwezera mbale wanu ndithu. Ndipo ngati mbale wanu sakhala pafupi ndi inu, kapena mukapanda kumdziwa, mubwere nayo kwanu kunyumba yanu, kuti ikhale kwanu, kufikira mbale wanu akaifuna, ndipo wambwezera iyo. Mutero nayenso bulu wake; mutero nachonso chovala chake, mutero nachonso chotayika chilichonse cha mbale wanu, chakumtayikira mukachipeza ndi inu; musamazilekerera. Mukapenya bulu kapena ng'ombe ya mbale wanu, zitagwa m'njira, musamazilekerera; mumthandize ndithu kuziutsanso. Mkazi asavale chovala cha mwamuna, kapena mwamuna asavale chovala cha mkazi; pakuti aliyense wakuchita izi Yehova Mulungu wanu anyansidwa naye. Mukachipeza chisa cha mbalame panjira, mumtengo kapena panthaka pansi, muli ana kapena mazira, ndi make alikuumatira ana kapena mazira, musamatenga make pamodzi ndi ana; muloletu make amuke, koma mudzitengere ana; kuti chikukomereni, ndi kuti masiku anu achuluke. Pamene mumanga nyumba yatsopano, muzimanga kampanda pa tsindwi lake, kuti ungatengere nyumba yanu mwazi, akagwako munthu. Musamabzala mbeu zosiyana m'munda wanu wamphesa, kuti zingaipsidwe mbeu zonse udazibzala, ndi zipatso za munda wamphesa zomwe. Musamalima ndi bulu ndi ng'ombe zikoke pamodzi. Musamavala nsalu yosokonezeka yaubweya pamodzi ndi thonje. Mudzipangire mphonje pangodya zinai za chofunda chanu chimene mudzifunda nacho. Munthu akatenga mkazi, nalowana naye, namuda, namneneza zoutsa mbiri yamanyazi, ndi kumveketsa dzina loipa, ndi kuti, Ndinamtenga mkazi uyu, koma polowana naye sindinapeza zizindikiro zakuti ndiye namwali ndithu; pamenepo atate wa namwaliyo ndi mai wake azitenga ndi kutuluka nazo zizindikiro za unamwali wake wa namwaliyo, kunka nazo kwa akulu a mudzi kuchipata; ndipo atate wa namwaliyo azinena kwa akulu, Ndinampatsa munthuyu mwana wanga wamkazi akhale mkazi wake, koma amuda; ndipo, taonani, wamneneza zoutsa mbiri yamanyazi, ndi kuti, Sindinapeza zizindikiro za unamwali wake m'mwana wako wamkazi; koma si izi zizindikiro za unamwali wa mwana wanga wamkazi. Ndipo azifunyulula chovalacho pamaso pa akulu a mudziwo. Pamenepo akulu a mudziwo azitenga munthuyu ndi kumkwapula; ndi kumlipitsa masekeli makumi okhaokha khumi a siliva, ndi kuipereka kwa atate wa namwaliyo, popeza anamveketsa dzina loipa namwali wa Israele, ndipo azikhala mkazi wake, sakhoza kumchotsa masiku ake onse. Koma chikakhala choona ichi, kuti zizindikiro zakuti ndiye namwali zidamsowa namwaliyo; pamenepo azimtulutsa namwaliyo ku khomo la nyumba ya atate wake, ndipo amuna a mudzi wake azimponya miyala kuti afe; popeza anachita chopusa m'Israele, kuchita chigololo m'nyumba ya atate wake; chotero uzichotsa choipacho pakati panu. Akampeza munthu alikugona ndi mkazi wokwatibwa ndi mwamuna; afe onse awiri, mwamuna wakugona ndi mkazi, ndi mkazi yemwe; chotero muzichotsa choipacho mwa Israele. Pakakhala namwali, wosadziwa mwamuna, wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, ndipo anampeza m'mudzi mwamuna, nagona naye; muziwatulutsa onse awiri kunka nao ku chipata cha mudzi uwo, ndi kuwaponya miyala kuti afe; namwaliyo popeza sanafuule angakhale anali m'mudzi; ndi mwamuna popeza anachepetsa mkazi wa mnansi wake; chotero muzichotsa choipacho pakati panu. Koma mwamuna akapeza namwali wopalidwa bwenzi kuthengo, namgwira mwamunayo, nagona naye; pamenepo afe mwamuna yekha wogona naye; koma namwaliyo musamamchitira kanthu; namwaliyo alibe tchimo loyenera imfa; pakuti mlandu uwu ukunga munthu waukira mnzake namupha; pakuti anampeza kuthengo; namwali wopalidwa bwenziyo anafuula, koma panalibe wompulumutsa. Munthu akapeza namwali wosadziwa mwamuna, ndiye wosapalidwa ubwenzi, nakamgwira nagona naye, napezedwa iwo, pamenepo mwamuna amene anagona naye azipatsa atate wake wa namwaliyo masekeli makumi asanu a siliva, ndipo azikhala mkazi wake; popeza anamchepetsa; sakhoza kumchotsa masiku ake onse. Munthu asatenge mkazi wa atate wake, kapena kuvula atate wake. Munthu wophwetekwa, wophwanyika kapena wofulika, asalowe m'msonkhano wa Yehova. Mwana wa m'chigololo asalowe m'msonkhano wa Yehova, ngakhale mbadwo wake wakhumi usalowe m'msonkhano wa Yehova. Mwamoni kapena Mmowabu asalowe m'msonkhano wa Yehova; ngakhale mbadwo wao wakhumi usalowe m'msonkhano wa Yehova, ku nthawi zonse; popeza sanakumana nanu ndi mkate ndi madzi m'njira muja munatuluka m'Ejipito; popezanso anakulembererani Balamu mwana wa Beori wa ku Petori wa Mesopotamiya, kuti akutemberereni. Ndipo Yehova Mulungu wanu sanafune kumvera Balamu; koma Yehova Mulungu wanu anakusandulizirani tembererolo likhale mdalitso, popeza Yehova Mulungu wanu anakukondani. Musawafunira mtendere, kapena chowakomera masiku anu onse ku nthawi zonse. Musamanyansidwa naye Mwedomu, popeza ndiye mbale wanu; musamanyansidwa naye Mwejipito, popeza munali alendo m'dziko lake. Ana obadwa nao a mbadwo wachitatu alowe m'msonkhano wa Yehova. Nkhondo yanu ikatuluka pa adani anu, mudzisunge kusachita choipa chilichonse. Pakakhala munthu pakati pa inu, ndiye wosayera chifukwa chochitika usiku, azituluka kunja kwa chigono, asalowe pakati pa chigono; koma kudzali pofika madzulo, asambe m'madzi; ndipo litalowa dzuwa alowe pakati pa chigono. Mukhale nao malo kunja kwa chigono kumene muzimukako kuthengo; nimukhale nacho chokumbira mwa zida zanu; ndipo kudzali, pakukhala inu pansi kuthengo mukumbe nacho, ndi kutembenuka ndi kufotsera chakutulukacho; popeza Yehova Mulungu wanu ayenda pakati pa chigono chanu kukupulumutsani ndi kupereka adani anu pamaso panu; chifukwa chake chigono chanu chikhale chopatulika; kuti angaone kanthu kodetsa mwa inu, ndi kukupotolokerani. Musamapereka kwa mbuye wake kapolo wopulumuka kwa mbuye wake kuthawira kwa inu; akhale nanu, pakati panu, ku malo asankhako iye m'mudzi mwanu mwina momkonda; musamamsautsa. Pasakhale mkazi wachigololo pakati pa ana akazi a Israele, kapena wachigololo pakati pa ana amuna a Israele. Musamabwera nayo mphotho ya wachigololo, kapena mtengo wake wa galu kulowa nazo m'nyumba ya Yehova Mulungu wanu, chifukwa cha chowinda chilichonse; pakuti onse awiriwa Yehova Mulungu wanu anyansidwa nao. Musamakongoletsa mbale wanu mopindulitsa; phindu la ndalama, phindu la chakudya, phindu la kanthu kalikonse kokongoletsa. Mukongoletse mlendo mopindulitsa; koma mbale wanu musamamkongoletsa mopindulitsa, kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni mwa zonse muzigwira ndi dzanja lanu, m'dziko limene mulowamo kulilandira. Mukawindira Yehova Mulungu wanu chowinda, musamachedwa kuchichita; popeza Yehova Mulungu wanu adzakufunsani za ichi ndithu ndipo mukadachimwako. Koma mukapanda kulonjeza chowinda, mulibe kuchimwa. Chotuluka pa milomo yanu muchisamalire ndi kuchichita; monga munalonjezera Yehova Mulungu wanu, chopereka chaufulu munachilonjeza pakamwa panu. Mukalowa m'munda wamphesa wa mnansi wanu, mudyeko mphesa ndi kukhuta nazo monga mufuna eni; koma musaika kanthu m'chotengera chanu. Mukalowa m'tirigu wosasenga wa mnansi wanu, mubudule ngala ndi dzanja lanu, koma musasengako ndi chisenga tirigu wachilili wa mnansi wanu. Munthu akatenga mkazi akhale wake, kudzali, ngati sapeza ufulu pamaso pake, popeza anapeza mwa iye kanthu kosayenera, amlembere kalata wa chilekanitso, ndi kumpereka uyu m'dzanja lake, ndi kumtulutsa m'nyumba mwake. Ndipo atatuluka m'nyumba mwake, amuke nakhale mkazi wa mwamuna wina. Ndipo akamuda mwamuna wachiwiriyo, nakamlemberanso kalata wa chilekanitso, ndi kumpereka uyu m'dzanja lake, nakamtulutsa m'nyumba mwake; kapena akamwalira mwamuna wotsirizayo, amene anamtenga akhale mkazi wake; pamenepo mwamuna woyamba anamchotsayo sangathe kumtenganso akhale mkazi wake, atadetsedwa iye; pakuti ichi ndi chonyansa pamaso pa Yehova; ndipo usamachimwitsa dziko, limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholandira chanu. Munthu akatenga mkazi watsopano, asatuluke nayo nkhondo, kapena asamchititse kanthu kalikonse; akhale waufulu kunyumba yake chaka chimodzi, nakondweretse mkazi adamtengayo. Munthu asalandire chikole mphero, ngakhale mwanamphero, popeza alandirapo chikole moyo wa munthu. Akampeza munthu waba mbale wake wina wa ana a Israele, namuyesa kapolo, kapena wamgulitsa, afe wakubayo; potero muzichotsa choipacho pakati panu. Chenjerani nayo nthenda yakhate, kusamaliratu, ndi kuchita monga mwa zonse akuphunzitsani ansembe Alevi; monga ndinalamulira iwo, momwemo muzisamalira kuchita. Kumbukirani chimene Yehova Mulungu wanu anachitira Miriyamu panjira, potuluka inu m'dziko la Ejipito. Mukakongoletsa mnansi wanu ngongole iliyonse, musamalowa m'nyumba mwake kudzitengera chikole chake. Muime pabwalo, ndi munthu amene umkongoletsayo azituluka nacho chikolecho kwa inu muli pabwalo. Ndipo akakhala munthu waumphawi musagone muli nacho chikole chake; polowa dzuwa mumbwezeretu chikolecho, kuti agone m'chovala chake, ndi kukudalitsani; ndipo kudzakukhalirani chilungamo pamaso pa Yehova Mulungu wanu. Musamasautsa wolembedwa ntchito, wakukhala waumphawi ndi wosauka, wa abale anu kapena wa alendo ali m'dziko mwanu, m'midzi mwanu. Pa tsiku lake muzimpatsa kulipira kwake, lisalowepo dzuwa; pakuti ndiye waumphawi, ndi mtima wake ukhumba uku; kuti angakulirireni kwa Yehova, ndipo kukukhalireni tchimo. Atate asaphedwere ana, ndi ana asaphedwere atate; munthu yense aphedwere tchimo lakelake. Musamaipsa mlandu wa mlendo, kapena wa ana amasiye; kapena kutenga chikole chovala cha mkazi wamasiye; koma muzikumbukira kuti munali akapolo m'Ejipito, ndi kuti Yehova Mulungu wanu anakuombolaniko; chifukwa chake ndikuuzani kuchita chinthu ichi. Mutasenga dzinthu zanu m'munda mwanu, ndipo mwaiwala mtolo m'mundamo, musabwererako kuutenga; ukhale wa mlendo, wa mwana wamasiye, ndi wa mkazi wamasiye; kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni m'ntchito zonse za manja anu. Mutagwedeza mtengo wanu wa azitona musayesenso nthambi mutatha nazo; akhale a mlendo, a mwana wamasiye, ndi a mkazi wamasiye. Mutatchera m'munda wanu wamphesa, musakunkha pambuyo panu; zikhale za mlendo, za mwana wamasiye, ndi za mkazi wamasiye. Ndipo muzikumbukira kuti munali akapolo m'dziko la Ejipito; chifukwa chake ndikuuzani kuchita chinthu ichi. Pakakhala ndeu pakati pa anthu, nakapita kukaweruzidwa iwowa, nakaweruza mlandu wao oweruza; azimasula wolungama, namange woipa. Ndipo kudzali, wochita choipa akayenera amkwapule, woweruza amgonetse kuti amkwapule pamaso pake, amwerengere zofikira choipa chake. Amkwapule kufikira makumi anai, asaonjezepo; pakuti, akaonjezapo ndi kumkwapula mikwapulo yambiri, angapeputse mbale wanu pamaso panu. Musamapunamiza ng'ombe popuntha tirigu. Abale akakhala pamodzi, nafa wina wa iwowa, wopanda mwana wamwamuna, mkazi wa wakufayo asakwatibwe ndi mlendo wakunja; mbale wa mwamuna wake alowane naye, namtenge akhale mkazi wake, namchitire zoyenera mbale wa mwamuna wake. Ndipo kudzali, kuti woyamba kubadwa amene adzambala, adzalowa dzina lake la mbale wake wakufayo, kuti dzina lake lisafafanizidwe m'Israele. Ndipo ngati mwamunayo safuna kutenga mkazi wa mbale wake, mkazi wa mbale wakeyo azikwera kunka kuchipata, kwa akulu, ndi kuti, Mbale wa mwamuna wanga akana kuutsira mbale wake dzina m'Israele; safuna kundichitira ine zoyenera mbale wa mwamuna. Pamenepo akulu a mudzi wake amuitane, ndi kulankhula naye; ndipo akaimirira ndi kuti, Sindifuna kumtenga; pamenepo mkazi wa mbale wake azimyandikiza pamaso pa akulu, nachotse nsapato yake ku phazi la mwamunayo, ndi kumthira malovu pankhope pake, ndi kumyankha ndi kuti, Atere naye mwamuna wosamanga nyumba ya mbale wake. Ndipo azimutcha dzina lake m'Israele, Nyumba ya uje anamchotsa nsapato. Akalimbana wina ndi mnzake, nakayandikiza mkazi wa winayo kulanditsa mwamuna wake m'dzanja la wompandayo, nakatulutsa dzanja lake, ndi kumgwira kudzivalo; pamenepo muzidula dzanja lake; diso lanu lisamchitire chifundo. Musamakhala nayo m'thumba mwanu miyala ya miyeso iwiri, waukulu ndi waung'ono. Musamakhala nayo m'nyumba yanu miyeso ya efa yosiyana, waukulu ndi waung'ono. Muzikhala nao mwala wa muyeso wofikira ndi woyenera; mukhale nao muyeso wa efa wofikira ndi woyenera; kuti masiku anu achuluke m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani. Pakuti onse akuchita zinthu izi, onse akuchita chisalungamo, Yehova Mulungu wanu anyansidwa nao. Kumbukirani chochitira inu Amaleke panjira, potuluka inu m'Ejipito; kuti anakomana ndi inu panjira, nakantha onse ofooka akutsala m'mbuyo mwanu, pakulema ndi kutopa inu; ndipo sanaope Mulungu. Ndipo kudzali, pamene Yehova Mulungu wanu atakupumulitsirani adani anu onse ozungulira, m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanuchanu, kuti muzifafaniza chikumbutso cha Amaleke pansi pa thambo; musamaiwala. Ndipo kudzali, utakalowa m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanu, ndipo mwachilandira ndi kukhala m'mwemo; kuti muzitengako zoyamba za zipatso zonse za nthaka, zakubwera nazo inu zochokera m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani; ndi kuziika mudengu, ndi kupita ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake. Ndipo mufike kwa wansembe wakukhala m'masiku awa, ndi kunena naye, Ndivomereza lero lino kwa Yehova Mulungu wako, kuti ndalowa m'dziko limene Yehova analumbirira makolo athu, kuti adzatipatsa ili. Ndipo wansembe alandire dengu m'manja mwanu, ndi kuuika pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu. Ndipo muyankhe ndi kuti pamaso pa Yehova Mulungu wanu, Kholo langa ndiye Mwaramu wakuti atayike, natsika kunka ku Ejipito, nagoneragonera komweko ali nao anthu pang'ono, nasandukako mtundu waukulu, wamphamvu, ndi wochuluka anthu ake; koma Aejipito anatichitira choipa, natizunza, natisenza ntchito yolimba. Pamenepo tinafuulira kwa Yehova, Mulungu wa makolo athu; ndipo Yehova anamva mau athu, napenya kuzunzika kwathu, ndi ntchito yathu yolemetsa, ndi kupsinjika kwathu; ndipo Yehova anatitulutsa m'Ejipito ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi kuopsa kwakukulu, ndi zizindikiro, ndi zodabwitsa; ndipo anabwera nafe kumalo kuno, natipatsa dziko ili ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi. Ndipo tsopano, taonani, ndabwera nazo zoyamba za zipatso za nthaka, zimene Inu, Yehova, mwandipatsa. Ndipo muziike pamaso pa Yehova Mulungu wanu; ndipo mukondwere nazo zokoma zonse zimene Yehova Mulungu wanu akupatsani, inu ndi nyumba zanu, inu ndi Mlevi, ndi mlendo ali pakati panu. Mutatha kugawa magawo khumi, zobala zanu zonse chaka chachitatu, ndicho chaka chogawa magawo khumi, muzizipereka kwa Mlevi, kwa mlendo, kwa mwana wamasiye, ndi kwa mkazi wamasiye, kuti adye m'midzi mwanu, ndi kukhuta. Ndipo munene pamaso pa Yehova Mulungu wanu, Ndachotsa zopatulika m'nyumba mwanga, ndi kuzipereka kwa Mlevi, ndi kwa mlendo, ndi kwa mwana wamasiye, ndi kwa mkazi wamasiye, monga mwa lamulo lanu lonse munandilamulira ine; sindinalakwira malamulo anu, kapena kuwaiwala. Sindinadyako m'chisoni changa, kapena kuchotsako podetsedwa, kapena kuperekako kwa akufa; ndamvera mau a Yehova Mulungu wanga; ndachita monga mwa zonse munandilamulira ine. Penyani muli mokhalamo mwanu mopatulika, m'mwamba, ndipo dalitseni anthu anu Israele, ndi nthaka imene munatipatsa, monga munalumbirira makolo athu, dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi. Lero lino Yehova Mulungu wanu akulamulirani kuchita malemba ndi maweruzo awa; potero muzimvera ndi kuwachita ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse. Mwalonjezetsa Yehova lero kuti adzakhala Mulungu wanu, ndi kuti mudzayenda m'njira zake, ndi kusunga malemba ake, ndi malamulo ake, ndi maweruzo ake, ndi kumvera mau ake. Ndipo Yehova wakulonjezetsani lero kuti mudzakhala anthu akeake a pa okha, monga ananena ndi inu, ndi kuti mudzasunga malamulo ake onse; kuti akukulitseni koposa amitundu onse anawalenga, wolemekezeka, womveka dzina, ndi waulemu; ndi kuti mukhale mtundu wa anthu wopatulikira Yehova Mulungu wanu monga ananena. Ndipo Mose ndi akulu a Israele anauza anthu, nati, Sungani malamulo onse ndikuuzani lero. Ndipo kudzali, tsiku lakuoloka inu Yordani kulowa dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, kuti mudziutsire miyala yaikulu, ndi kuimata ndi njeresa; ndipo mulemberepo mau onse a chilamulo ichi, mutaoloka; kuti mulowe m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, monga Yehova Mulungu wa makolo anu ananena ndi inu. Ndipo kudzali, mutaoloka Yordani, muutse miyala iyi ndikuuzani lero, m'phiri la Ebala, ndi kuimata ndi njeresa. Ndipo komweko mumangire Yehova Mulungu wanu guwa la nsembe, guwa la nsembe lamiyala; musakwezepo pangizo chachitsulo. Mumange guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu lamiyala yosasema; ndi kuperekapo nsembe zopsereza kwa Yehova Mulungu wanu; ndi kuphera nsembe zoyamika, ndi kudyapo, ndi kukondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu. Ndipo mulembere pa miyalayi mau onse a chilamulo ichi mopenyeka bwino. Ndipo Mose, ndi ansembe Alevi ananena ndi Israele wonse, ndi kuti, Khalani chete, imvanitu, Israele; lero lino mwasanduka mtundu wa anthu wa Yehova Mulungu wanu. Potero muzimvera mau a Yehova Mulungu wanu, ndi kuchita malamulo ake ndi malemba ake, amene ndikuuzani lero lino. Ndipo Mose anauza anthu tsiku lomwelo, ndi kuti, Aimirire awa pa phiri la Gerizimu kudalitsa anthu, mutaoloka Yordani: Simeoni ndi Levi, ndi Yuda, ndi Isakara, ndi Yosefe, ndi Benjamini. Naimirire awa pa phiri la Ebala, kutemberera: Rubeni, Gadi, ndi Asere, ndi Zebuloni, Dani ndi Nafutali. Ndipo ayankhe Alevi ndi kunena kwa amuna onse a Israele, ndi mau omveka. Wotembereredwa munthu wakupanga fano losema kapena loyenga, lonyansidwa nalo Yehova, ntchito ya manja a mmisiri, ndi kuliika m'malo a m'tseri. Ndipo anthu onse ayankhe ndi kuti, Amen. Wotembereredwa iye wakupeputsa atate wake kapena mai wake. Ndi anthu onse anene, Amen. Wotembereredwa iye wakusendeza malire a mnansi wake. Ndi anthu onse anene, Amen. Wotembereredwa wakusokeretsa wakhungu m'njira. Ndi anthu onse anene, Amen. Wotembereredwa iye wakuipsa mlandu wa mlendo, mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye. Ndi anthu onse anene, Amen. Wotembereredwa iye wakugona ndi mkazi wa atate wake; popeza wavula atate wake. Ndi anthu onse anene, Amen. Wotembereredwa iye wakugona ndi nyama iliyonse. Ndi anthu onse anene, Amen. Wotembereredwa iye wakugona ndi mlongo wake, mwana wamkazi wa atate wake, kapena mwana wamkazi wa make. Ndi anthu onse anene, Amen. Wotembereredwa iye wakugona ndi mpongozi wake. Ndi anthu onse anene, Amen. Wotembereredwa iye wakukantha mnansi wake m'tseri. Ndi anthu onse anene, Amen. Wotembereredwa iye wakulandira chamwazi chakuti akanthe munthu wosachimwa. Ndi anthu onse anene, Amen. Wotembereredwa iye wosavomereza mau a chilamulo ichi kuwachita. Ndi anthu onse anene, Amen. Ndipo kudzali, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu mwachangu, ndi kusamalira kuchita malamulo ake onse amene ndikuuzani lero, kuti Yehova Mulungu wanu adzakukulitsani koposa amitundu onse a pa dziko lapansi; ndipo madalitso awa onse adzakugwerani, ndi kukupezani, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu. Mudzakhala odala m'mudzi, ndi odala kubwalo. Zidzakhala zodala zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, ndi zipatso za zoweta zanu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi zoswana za nkhosa zanu. Lidzakhala lodala dengu lanu, ndi choumbiramo mkate wanu. Mudzakhala odala polowa inu, mudzakhala odala potuluka inu. Yehova adzakantha adani anu akukuukirani; adzakudzerani njira imodzi, koma adzathawa pamaso panu njira zisanu ndi ziwiri. Yehova adzakulamulirani dalitso m'nkhokwe zanu, ndi m'zonse mutulutsirako dzanja lanu; ndipo adzakudalitsani m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani. Yehova adzakukhazikirani yekha mtundu wa anthu wopatulika, monga anakulumbirirani; ngati mudzasunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m'njira zake. Ndipo anthu onse a pa dziko lapansi adzaona kuti akutchulani dzina la Yehova; nadzakuopani. Ndipo Yehova adzakuchulukitsirani zokoma, m'zipatso za thupi lanu, ndi m'zipatso za zoweta zanu, ndi m'zipatso za nthaka yanu, m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani ilo. Yehova adzakutsegulirani chuma chake chokoma, ndicho thambo la kumwamba, kupatsa dziko lanu mvula m'nyengo yake, ndi kudalitsa ntchito zonse za dzanja lanu; ndipo mudzakongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha. Ndipo Yehova adzakuyesani mutu, si mchira ai; ndipo mudzakhala wa pamwamba pokha, si wapansi ai; ngati mudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu, amene ndikuuzani lero, kuwasunga ndi kuwachita; osapatukira mau ali onse ndikuuzani lero, kulamanja, kapena kulamanzere, kutsata milungu ina kuitumikira. Koma kudzali, mukapanda kumvera mau a Yehova Mulungu wanu, kusamalira kuchita malamulo ake onse ndi malemba ake amene ndikuuzani lero, kuti matemberero awa onse adzakugwerani ndi kukupezani. Mudzakhala otembereredwa m'mudzi, ndi otembereredwa pabwalo. Lidzakhala lotembereredwa dengu lanu ndi choumbiramo mkate wanu. Zidzakhala zotembereredwa zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi zoswana za nkhosa zanu. Mudzakhala otembereredwa polowa inu, ndi otembereredwa potuluka inu. Yehova adzakutumizirani temberero, chisokonezeko, ndi kudzudzula monsemo mukatulutsa dzanja lanu kuchita kanthu, kufikira mwaonongeka, kufikira mwatayika msanga, chifukwa cha zochita inu zoipa, zimene wandisiya nazo. Yehova adzakumamatiritsani mliri, kufikira akakuthani kukuchotsani kudziko, kumene mupitako kulilandira. Yehova adzakukanthani ndi nthenda yoondetsa ya chifuwa, ndi malungo, ndi chibayo, ndi kutentha thupi, ndi lupanga, chinsikwi ndi chinoni; ndipo zidzakutsatani kufikira mwatayika. Ndipo thambo lanu la pamwamba pamutu panu lidzakhala ngati mkuwa, ndi dziko lili pansi panu ngati chitsulo. Yehova adzasanduliza mvula ya dziko lanu ikhale fumbi ndi phulusa; zidzakutsikirani kuchokera kumwamba, kufikira mwaonongeka. Yehova adzalola adani anu akukantheni; mudzawatulukira njira imodzi, koma mudzawathawa pamaso pao njira zisanu ndi ziwiri, ndipo mudzagwedezeka pakati pa maufumu onse a dziko lapansi. Ndipo mitembo yanu idzakhala chakudya cha mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi zilombo zonse za pa dziko lapansi, ndipo palibe wakuziingitsa. Yehova adzakukanthani ndi zilombo za ku Ejipito, ndi nthenda yotuluka mudzi, ndi chipere, ndi mphere, osachira nazo. Yehova adzakukanthani ndi misala, ndi khungu, ndi kuzizwa mumtima; ndipo mudzafufuza usana, monga wakhungu amafufuza mumdima, ndipo simudzapindula nazo njira zanu; koma mudzakhala wopsinjika, nadzakuberani masiku onse, wopanda wina wakukupulumutsani. Mudzapalana ubwenzi ndi mkazi, koma mwamuna wina adzagona naye; mudzamanga nyumba, osakhala m'mwemo; mudzaoka munda wamphesa, osalawa zipatso zake. Adzapha ng'ombe yanu, pamaso panu, osadyako inu; adzalanda bulu wanu molimbana pamaso panu, osakubwezerani; adzapereka nkhosa zanu kwa adani anu, wopanda wina wakukupulumutsani. Adzapereka ana anu aamuna ndi aakazi kwa anthu a mtundu wina, ndipo m'maso mwanu mudzada ndi kupenyerera, powalirira tsiku lonse; koma mulibe mphamvu m'dzanja lanu. Mtundu wa anthu umene simudziwa udzadya zipatso za nthaka yanu ndi ntchito zanu zonse; ndipo mudzakhala wopsinjika ndi wophwanyika masiku onse; nimudzakhala oyeruka chifukwa chomwe muchiona ndi maso anu. Yehova adzakukanthani ndi chilonda choipa chosachira nacho kumaondo, ndi kumiyendo, kuyambira pansi pa phazi lanu kufikira pamwamba pa mutu panu. Yehova adzamukitsa inu, ndi mfumu yanu imene mudzadziikira, kwa mtundu wa anthu umene simudziwa, inu kapena makolo anu; ndipo mudzatumikirako milungu ina ya mitengo ndi miyala. Ndipo mudzakhala chodabwitsa, ndi nkhani, ndi nthanthi, mwa mitundu yonse ya anthu amene Yehova akutsogoleraniko. Mudzatuluka nazo mbeu zambiri kumunda, koma mudzakolola pang'ono; popeza dzombe lidzazitha. Mudzaoka m'minda yamphesa ndi kuilima, koma osamwa vinyo wake, kapena kutchera mphesa zake, popeza mbozi zidzaidya. Mudzakhala nayo mitengo ya azitona m'malire anu onse, osadzola mafuta; popeza zipatso za mitengo ya azitona zidzapululuka. Mudzabala ana aamuna ndi aakazi, osakhala nao, popeza adzalowa ukapolo. Mitengo yanu yonse ndi zipatso za nthaka yanu zidzakhala zaozao za dzombe. Mlendo wokhala pakati panu adzakulirakulira inu, koma inu mudzacheperachepera. Iye adzakukongoletsani, osamkongoletsa ndinu; iye adzakhala mutu, koma inu ndinu mchira. Ndipo matemberero awa onse adzakugwerani, nadzakulondolani, ndi kukupezani, kufikira mwaonongeka, popeza simunamvera mau a Yehova Mulungu wanu, kusunga malamulo ake ndi malemba ake amene anakulamulirani; ndipo zidzakukhalirani inu ndi mbeu zanu ngati chizindikiro ndi chozizwa, nthawi zonse. Popeza simunatumikira Yehova Mulungu wanu ndi chimwemwe ndi mokondwera mtima, chifukwa cha kuchuluka zinthu zonse; chifukwa chake mudzatumikira adani anu amene Yehova adzakutumizirani, ndi njala, ndi ludzu, ndi usiwa, ndi kusowa zinthu zonse; ndipo adzaika goli lachitsulo pakhosi panu, kufikira atakuonongani. Yehova adzakutengerani mtundu wa anthu wochokera kutali ku malekezero a dziko lapansi, monga iuluka mphungu; mtundu wa anthu amene simunamva malankhulidwe ao; mtundu wa anthu wa nkhope yaukali, wosamalira nkhope ya wokalamba, wosamchitira chifundo mwana; ndipo adzadya zipatso za ng'ombe zanu, ndi zipatso za nthaka yanu, kufikira mwaonongeka; osakusiyirani tirigu, vinyo, kapena mafuta, zoswana ng'ombe zanu, zoswana nkhosa zanu, kufikira atakuonongani. Ndipo adzakuzingani m'midzi mwanu monse, kufikira adagwa malinga anu atali ndi olimba, amene munawakhulupirira, m'dziko lanu lonse; inde, adzakuzingani m'midzi mwanu monse, m'dziko lanu lonse limene Yehova Mulungu wanu akupatsani. Ndipo mudzadya chipatso cha thupi lanu, nyama ya ana anu aamuna ndi aakazi amene Yehova Mulungu wanu anakupatsani; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani adani anu. Mwamuna wololopoka nkhongono ndi wanyonga pakati pa inu, diso lake lidzaipira mbale wake, ndi mkazi wa pa mtima wake, ndi ana ake otsalira; osapatsako mmodzi yense wa iwowa nyama ya ana ake alinkudyayo, popeza sikamtsalira kanthu; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani mdani wanu m'midzi mwanu monse. Mkazi wololopoka nkhongono ndi wanyonga pakati pa inu, wosayesa kuponda pansi ndi phazi lake popeza ndiye wanyonga, ndi wololopoka nkhongono, diso lake lidzamuipira mwamuna wa pamtima pake, ndi mwana wake wamwamuna ndi wamkazi; ndicho chifukwa cha matenda akutuluka pakati pa mapazi ake, ndi ana ake adzawabala; popeza adzawadya m'tseri posowa zinthu zonse; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani mdani wanu m'midzi mwanu. Mukapanda kusamalira kuchita mau onse a chilamulo ichi olembedwa m'buku ili, kuopa dzina ili la ulemerero ndi loopsa, ndilo Yehova Mulungu wanu; Yehova adzachita miliri yanu ndi ya ana anu ikhale yodabwitsa, miliri yaikulu ndi yokhalitsa, ndi nthenda zoipa ndi zokhalitsa. Ndipo adzakubwezerani nthenda zonse za Ejipito, zimene munaziopa; ndipo zidzakumamatirani inu. Ndiponso nthenda zonse ndi miliri yonse zosalembedwa m'buku la chilamulo ichi, Yehova adzakutengerani izi, kufikira mwaonongeka. Ndipo mudzatsala anthu pang'ono, mungakhale mudachuluka ngati nyenyezi za m'mwamba; popeza simunamvera mau a Yehova Mulungu wanu. Ndipo kudzali kuti, monga Yehova anakondwera nanu kukuchitirani zabwino, ndi kukuchulukitsani; momwemo Yehova adzakondwera nanu kutayikitsa ndi kuononga inu, ndipo adzakuzulani kudziko kumene mulowako kulilandira. Ndipo Yehova adzakubalalitsani mwa mitundu yonse ya anthu, kuyambira malekezero a dziko lapansi kufikira malekezero a dziko lapansi; ndipo kumeneko mudzatumikira milungu ina, imene simunaidziwa, inu ndi makolo anu, yamitengo ndi yamiyala. Ndipo mwa a mitundu iyi simudzapumula, inde sipadzakhala popumulira phazi lanu; koma Yehova adzakupatsani kumeneko mtima wonjenjemera, m'maso mwanu mudzada, mudzafa ndi kulefuka mtima. Ndipo moyo wanu udzakhala wanjiranjira pamaso panu, ndipo mudzachita mantha usiku ndi usana, osakhazika mtima za moyo wanu. M'mawa mudzati, Mwenzi atafika madzulo! Ndi madzulo mudzati, Mwezi utafika m'mawa! Chifukwa cha mantha a m'mtima mwanu amene mudzaopa nao, ndi chifukwa cha zopenya maso anu zimene mudzazipenya. Ndipo Yehova adzakubwezerani ku Ejipito ndi ngalawa, pa njira imene ndinati kwa inu, kuti, Simudzaionanso; ndipo kumeneko mudzadzigulitsa kwa adani anu mukhale akapolo ndi adzakazi; koma palibe wogula inu. Awa ndi mau a chipangano chimene Yehova analamulira Mose achichite ndi ana a Israele m'dziko la Mowabu, pamodzi ndi chipanganocho anachita nao m'Horebu. Ndipo Mose anaitana Israele wonse, nati nao, Munapenya inu zonse zimene Yehova anachitira Farao, ndi anyamata ake onse, ndi dziko lake lonse, pamaso panu m'dziko la Ejipito; mayesero akuluwa maso anu anawapenya, zizindikirozo, ndi zozizwa zazikulu zija; koma Yehova sanakupatseni mtima wakudziwa, ndi maso akupenya, ndi makutu akumva, kufikira lero lino. Ndipo ndinakutsogolerani zaka makumi anai m'chipululu; zovala zanu sizinatha pathupi panu, ndi nsapato zanu sizinatha pa phazi lanu. Simunadya mkate, simunamwa vinyo kapena chakumwa cholimba; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu. Ndipo pamene munafika pamalo pano, Sihoni mfumu ya Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya Basani, anatuluka kudzakomana nafe kunkhondo, ndipo tinawakantha; ndipo tinalanda dziko lao, ndi kulipereka likhale cholowa chao cha Arubeni, ndi Agadi, ndi fuko la hafu la Manase. Chifukwa chake sungani mau a chipangano ichi ndi kuwachita, kuti muchite mwanzeru m'zonse muzichita. Muimirira inu nonse lero lino pamaso pa Yehova Mulungu wanu; mafumu anu, mafuko anu, akulu anu, ndi akapitao anu, amuna onse a Israele, makanda anu, akazi anu, ndi mlendo wanu wakukhala pakati pa zigono zanu, kuyambira wotema nkhuni kufikira wotunga madzi; kuti mulowe chipangano cha Yehova Mulungu wanu, ndi lumbiriro lake, limene Yehova Mulungu wanu achita ndi inu lero lino; kuti adzikhazikire inu, mtundu wake wa anthu lero lino, ndi kuti akhale kwa inu Mulungu, monga ananena ndi inu, ndi monga analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo. Koma sindichita chipangano ichi ndi lumbiro ili ndi inu nokha; komanso ndi iye wakuimirira pano nafe lero lino pamaso pa Yehova Mulungu wathu, ndiponso ndi iye wosakhala pano nafe lero lino. Pakuti mudziwa chikhalidwe chathu m'dziko la Ejipito, ndi kuti tinapyola pakati pa amitundu amene munawapyola; ndipo munapenya zonyansa zao, ndi mafano ao, mtengo ndi mwala, siliva ndi golide, zokhala pakati pao; kuti angakhale pakati pa inu mwamuna, kapena mkazi, kapena banja, kapena fuko, mtima wao watembenuka kusiyana naye Yehova Mulungu wathu lero lino, kuti apite ndi kutumikira milungu ya amitundu aja; kuti ungakhale pakati pa inu muzu wakubala ndulu ndi chowawa. Ndipo kungakhale, akamva mau a lumbiro ili adzadzidalitsa m'mtima mwake, ndi kuti, Ndidzakhala nao mtendere, ndingakhale ndiyenda nao mtima wanga wopulukira, kuledzera nditamva ludzu; Yehova sadzamkhululukira, koma pamenepo mkwiyo wa Yehova ndi nsanje yake zidzamfukira munthuyo; ndipo temberero lonse lolembedwa m'buku ili lidzamkhalira; ndipo Yehova adzafafaniza dzina lake pansi pa thambo. Ndipo Yehova adzamsiyanitsa ndi mafuko onse a Israele ndi kumchitira choipa, monga mwa matemberero onse a chipangano cholembedwa m'buku ili la chilamulo. Ndipo mbadwo ukudza, ana anu akuuka mutafa inu, ndi mlendo wochokera ku dziko lakutali, adzati, pakuona iwo miliri ya dziko ili, ndi nthendazi, Yehova awadwalitsa nazo. Ndi kuti lidapsa dziko lake lonse ndi sulufure, ndi mchere, kuti sabzalamo, kapena siliphukitsa kanthu kapena sumerapo msipu, monga kupasula kwake kwa Sodomu ndi Gomora, Adima, ndi Zeboimu, imene Yehova anaipasula m'mkwiyo wake ndi ukali wake; inde amitundu onse adzati, Yehova anachitira dziko ili chotero chifukwa ninji? Nchiyani kupsa mtima kwakukulu kumene? Pamenepo adzati, popeza analeka chipangano cha Yehova, Mulungu wa makolo ao, chimene anachita nao pakuwatulutsa m'dziko la Ejipito; napita natumikira milungu ina, naigwadira, milungu imene sanaidziwa, imene sanawagawira; chifukwa chake Yehova anapsera mtima dziko ili kulitengera temberero lonse lolembedwa m'buku ili. Ndipo Yehova anawazula m'nthaka mwao mokwiya ndi mozaza, ndi m'ukali waukulu, nawaponya m'dziko lina, monga lero lino. Zinsinsi nza Yehova Mulungu wathu; koma zovumbuluka nza ife ndi ana athu kosatha, kuti tichite mau onse a chilamulo ichi. Ndipo kudzakhala, zikakugwerani zonsezi, mdalitso ndi temberero, ndinaikazi pamaso panu, ndipo mukazikumbukira mumtima mwanu mwa amitundu onse, amene Yehova Mulungu wanu anakupirikitsiraniko; nimukabwerera kwa Yehova Mulungu wanu, ndi kumvera mau ake, monga mwa zonse ndikuuzani lero lino, inu ndi ana anu, ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse; pamenepo Yehova Mulungu wanu adzauchotsa ukapolo wanu, ndi kukuchitirani chifundo; nadzabwera ndi kukumemezani mwa mitundu yonse ya anthu, kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsiraniko. Otayika anu akakhala ku malekezero a thambo, Yehova Mulungu wanu adzakumemezani kumeneko, nadzakutenganiko; ndipo Yehova Mulungu wanu adzakulowetsani m'dziko lidakhala laolao la makolo anu, nilidzakhala lanulanu; ndipo adzakuchitirani zokoma, ndi kukuchulukitsani koposa makolo anu. Ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudulani mtima wanu, ndi mtima wa mbeu zanu, kuti mukonde Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, kuti mukhale ndi moyo. Ndipo Yehova Mulungu wanu adzaika matemberero awa onse pa adani anu, ndi iwo akukwiya ndi inu, amene anakulondolani. Pamenepo mutembenuke ndi kumvera mau a Yehova, ndi kuchita malamulo ake onse amene ndikuuzani lero lino. Ndipo Yehova Mulungu wanu adzakuchulukitsirani ntchito zonse za dzanja lanu, zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za zoweta zanu, ndi zipatso za nthaka yanu, zikukomereni; popeza Yehova Mulungu wanu adzakondweranso kukuchitirani zokoma; monga anakondwera ndi makolo anu; ngati mudzamvera mau a Yehova Mulungu wanu, kuwasunga malamulo ake ndi malemba ake olembedwa m'buku la chilamulo ichi; ngati mudzabwerera kudza kwa Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse. Pakuti lamulo ili ndikuuzani lero lino, silikukanikani kulizindikira, kapena silikhala kutali. Silikhala m'mwamba, kuti mukati, Adzatikwerera m'mwamba ndani, ndi kubwera nalo kwa ife, ndi kutimvetsa ili, kuti tilichite? Ndipo silikhala tsidya la nyanja, kuti mukati, Adzatiolokera ndani tsidya la nyanja, ndi kutitengera ili, ndi kutimvetsa ili, kuti tilichite? Pakuti mauwa ali pafupifupi ndi inu, m'kamwa mwanu, ndi m'mtima mwanu, kuwachita. Tapenyani, ndaika pamaso panu lero lino moyo ndi zokoma, imfa ndi zoipa; popeza ndikuuzani lero kukonda Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zake, ndi kusunga malamulo ake ndi malemba ake ndi maweruzo ake, kuti mukakhale ndi moyo ndi kuchuluka, ndi kuti Yehova Mulungu wanu akakudalitseni m'dziko limene mulowako kulilandira. Koma mukatembenukira mtima wanu, osamvera inu, nimukacheteka, ndi kugwadira milungu ina ndi kuitumikira; ndikulalikirani inu lero, kuti mudzatayika ndithu, masiku anu sadzachuluka m'dziko limene muolokera Yordani kulowamo kulilandira. Ndichititsa mboni lero, kumwamba ndi dziko lapansi zitsutse inu; ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, mdalitso ndi temberero; potero, sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo, inu ndi mbeu zanu; kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mau ake, ndi kummamatira Iye, pakuti Iye ndiye moyo wanu, ndi masiku anu ochuluka; kuti mukhale m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, kuwapatsa ili. Ndipo Mose anamuka nanena mau awa kwa Israele wonse, nati nao, Ndine munthu wa zaka zana ndi makumi awiri lero lino; sindikhozanso kutuluka ndi kulowa; ndipo Yehova anati kwa ine, Sudzaoloka Yordani uyu. Yehova Mulungu wanu ndiye adzaoloka pamaso panu, Iye ndiye adzaononga amitundu awo pamaso panu, ndipo mudzawalandira. Yoswa ndiye adzakutsogolerani pooloka, monga ananena Yehova. Ndipo Yehova adzawachitira monga anachitira Sihoni ndi Ogi, mafumu a Aamori, ndi dziko lao limene analiononga. Yehova akadzawapereka pamaso panu, muziwachitira monga mwa lamulo lonse ndakuuzani. Khalani amphamvu, limbikani mitima, musamachita mantha, kapena kuopsedwa chifukwa cha iwowa; popeza Yehova Mulungu wanu ndiye amene amuka nanu; Iye sadzakusowani, kapena kukusiyani. Ndipo Mose anaitana Yoswa, nati naye pamaso pa Israele wonse, Khala wamphamvu, nulimbe mtima; pakuti udzalowa nao anthu awa m'dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kuwapatsa ilo; ndipo iwe udzawalandiritsa ilo. Ndipo Yehova, Iye ndiye amene akutsogolera; Iye adzakhala ndi iwe, Iye sadzakusowa kapena kukusiya; usamachita mantha, usamatenga nkhawa. Ndipo Mose analembera chilamulo ichi, nachipereka kwa ansembe, ana a Levi, akunyamula likasa la chipangano la Yehova, ndi kwa akulu onse a Israele. Ndipo Mose anawauza, ndi kuti, Pakutha pake pa zaka zisanu ndi ziwiri, pa nyengo yoikika ya m'chaka chakulekerera, pa chikondwerero cha Misasa; pakufika Israele wonse kuoneka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, m'malo amene adzasankha, muzilalikira chilamulo ichi pamaso pa Israele wonse, m'makutu mwao. Sonkhanitsani anthu, amuna ndi akazi ndi ana ang'ono, ndi mlendo wokhala m'midzi mwanu, kuti amve, ndi kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu, ndi kusamalira kuchita mau onse a chilamulo ichi; ndi kuti ana ao osadziwa amve, naphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu, masiku onse akukhala ndi moyo inu kudziko kumene muolokera Yordani kulilandira likhale lanulanu. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ayandikira masiku ako akuti uyenera kufa; kaitane Yoswa, nimuoneke m'chihema chokomanako, kuti ndimlangize. Namuka Mose ndi Yoswa, naoneka m'chihema chokomanako. Ndipo Yehova anaoneka m'chihema, m'mtambo njo; ndipo mtambo njo unaima pa khomo la chihema. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, udzagona tulo ndi makolo ako; ndi anthu awa adzauka, nadzatsata ndi chigololo milungu yachilendo ya dziko limene analowa pakati pake, nadzanditaya Ine, ndi kuthyola chipangano changa ndinapangana naocho. Pamenepo ndidzawapsera mtima tsiku ilo, ndipo ndidzawataya, ndi kuwabisira nkhope yanga, ndipo adzathedwa, ndi zoipa ndi zovuta zambiri zidzawafikira; kotero kuti adzati tsiku lija, Sizitifikira kodi zoipa izi popeza Mulungu wathu sakhala pakati pa ife? Koma Ine ndidzabisatu nkhope yanga tsiku lija chifukwa cha zoipa zonse adazichita; popeza anadzitembenukira milungu ina. Ndipo tsopano mudzilemberere nyimbo iyi, ndi kuphunzitsa ana a Israele iyi; muiike m'kamwa mwao, kuti nyimbo iyi indichitire mboni yotsutsa ana a Israele. Pakuti nditakalowetsa awa m'dziko limene ndinalumbirira makolo ao, moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ndipo atadya nakhuta, nanenepa, pamenepo adzatembenukira milungu ina, ndi kuitumikira, ndi kundipeputsa Ine, ndi kuthyola chipangano changa. Ndipo kudzakhala, zitawafikira zoipa ndi zovuta zambiri, nyimbo iyi idzachita mboni pamaso pao; popeza siidzaiwalika m'kamwa mwa mbeu zao; popeza ndidziwa zolingirira zao azichita lero lino, ndisanawalowetse m'dziko limene ndinalumbira. Potero Mose analembera nyimboyi tsiku lomweli, naiphunzitsa ana a Israele. Ndipo anauza Yoswa mwana wa Nuni, nati Khala wamphamvu, nulimbe mtima; pakuti udzalowa nao ana a Israele m'dziko limene ndinawalumbirira; ndipo Ine ndidzakhala ndi iwe. Ndipo kunali, Mose atatha kulembera mau a chilamulo ichi m'buku, kufikira atalembera onse, Mose anauza Alevi akunyamula likasa la chipangano la Yehova, ndi kuti, Landirani buku ili la chilamulo, nimuliike pambali pa likasa la chipangano la Yehova Mulungu wanu, likhale komweko mboni yakutsutsa inu. Pakuti ndidziwa kupikisana kwanu, ndi kupulukira kwanu; taonani, pokhala ndikali ndi moyo pamodzi ndi inu lero, mwapikisana ndi Yehova; koposa kotani nanga nditamwalira ine! Ndisonkhanitsire akulu onse a mafuko anu, ndi akapitao anu, kuti ndinene mau awa m'makutu mwao, ndi kuchititsa mboni kumwamba ndi dziko lapansi zitsutse iwo. Pakuti ndidziwa kuti nditamwalira ine mudzadziipsa ndithu, ndi kupatuka m'njira imene ndinakuuzani; ndipo chidzakugwerani choipa masiku otsiriza; popeza mudzachita choipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wake ndi ntchito za manja anu. Ndipo Mose ananena mau a nyimbo iyi m'makutu mwa msonkhano wonse wa Israele, kufikira adatha. Kumwamba kutchere khutu, ndipo ndidzanena; ndi dziko lapansi limve mau a m'kamwa mwanga. Chiphunzitso changa chikhale ngati mvula; maneno anga agwe ngati mame; ngati mvula yowaza pamsipu, ndi monga madontho a mvula pazitsamba. Pakuti ndidzalalika dzina la Yehova. Nenani kuti Mulungu wathu ndi wamkulu. Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; Iye ndiye wolungama ndi wolunjika. Anamchitira zovunda si ndiwo ana ake, chilema nchao; iwo ndiwo mbadwo wopulukira ndi wokhotakhota. Kodi mubwezera Yehova chotero, anthu inu opusa ndi opanda nzeru? Kodi si ndiye Atate wanu, Mbuye wanu; anakulengani, nakukhazikitsani? Kumbukirani masiku akale, zindikirani zaka za mibadwo yambiri; funsani atate wanu, adzakufotokozerani; akulu anu, adzakuuzani. Pamene Wam'mwambamwamba anagawira amitundu cholowa chao, pamene anagawa ana a anthu, anaika malire a mitundu ya anthu, monga mwa kuwerenga kwao kwa ana a Israele. Pakuti gawo la Yehova ndilo anthu ake; Yakobo ndiye muyeso wa cholowa chake. Anampeza m'dziko la mabwinja, m'chipululu cholira chopanda kanthu; anamzinga, anamlangiza, anamsunga ngati kamwana ka m'diso. Monga mphungu ikasula chisa chake, nikapakapa pa ana ake, Iye anayala mapiko ake, nawalandira, nawanyamula pa mapiko ake. Yehova yekha anamtsogolera, ndipo palibe mulungu wachilendo naye. Anamuyendetsa pa misanje ya dziko lapansi, ndipo anadya zipatso za m'minda; namyamwitsa uchi wa m'thanthwe, ndi mafuta m'mwala wansangalabwe; mafuta a mkaka wang'ombe, ndi mkaka wankhosa, ndi mafuta a anaankhosa, ndi nkhosa zamphongo za mtundu wa ku Basani, ndi atonde, ndi impso zonenepa zatirigu; ndipo munamwa vinyo, mwazi wamphesa. Koma Yesuruni anasanduka wonenepa, natazira; wasanduka wonenepa, wakula, wakuta ndi mafuta; pamenepo anasiya Mulungu amene anamlenga, napeputsa thanthwe la chipulumutso chake. Anamchititsa nsanje ndi milungu yachilendo, anautsa mkwiyo wake ndi zonyansa. Anaziphera nsembe ziwanda, si ndizo Mulungu ai; milungu yosadziwa iwo, yatsopano yofuma pafupi, imene makolo anu sanaiope. Mwaleka Thanthwe limene linakubalani, mwaiwala Mulungu amene anakulengani. Ndipo Yehova anachiona, nawanyoza, pakuipidwa nao ana ake amuna, ndi akazi. Ndipo Iye anati, Ndidzawabisira nkhope yanga, ndidzaona kutsiriza kwao; popeza iwo ndiwo mbadwo wopulukira, ana osakhulupirika iwo. Anautsa nsanje yanga ndi chinthu chosati Mulungu; anautsa mkwiyo wanga ndi zopanda pake zao. Ndidzautsa nsanje yao ndi iwo osakhala mtundu wa anthu; ndidzautsa mkwiyo wao ndi mtundu wa anthu opusa. Pakuti wayaka moto mu mkwiyo wanga, utentha kumanda kunsi ukutha dziko lapansi ndi zipatso zake, nuyatsa maziko a mapiri. Ndidzawaunjikira zoipa; ndidzawathera mivi yanga. Adzaonda nayo njala adzanyekeka ndi makala a moto, chionongeko chowawa; ndipo ndidzawatumizira mano a zilombo, ndi ululu wa zokwawa m'fumbi. Pabwalo lupanga lidzalanda, ndi m'zipinda mantha; lidzaononga mnyamata ndi namwali, woyamwa pamodzi ndi munthu waimvi. Ndinati, Ndikadawauzira ndithu, ndikadafafaniza chikumbukiro chao mwa anthu. Ndikadapanda kuopa mkwiyo wa pa mdani, angayese molakwa outsana nao, anganene, Lakwezeka dzanja lathu, ndipo Yehova sanachite ichi chonse. Popeza iwo ndiwo mtundu wa anthu wosowa uphungu konse, ndipo alibe chidziwitso. Akadakhala nazo nzeru, akadazindikira ichi, akadasamalira chitsirizo chao! Mmodzi akadapirikitsa zikwi, awiri akadathawitsa zikwi khumi, akadapanda kuwagulitsa Thanthwe lao, akadapanda kuwapereka Yehova. Popeza thanthwe lao nlosanga Thanthwe lathu, oweruza a pamenepo ndiwo adani athu. Pakuti mpesa wao ndiwo wa ku Sodomu, ndi wa m'minda ya ku Gomora; mphesa zao ndizo mphesa zandulu, matsangwi ao ngowawa. Vinyo wao ndiwo ululu wa zinjoka, ndi ululu waukali wa mphiri. Kodi sichisungika ndi Ine, cholembedwa chizindikiro mwa chuma changa chenicheni? Kubwezera chilango nkwanga, kubwezera komwe, pa nyengo ya kuterereka phazi lao; pakuti tsiku la tsoka lao layandika, ndi zinthu zowakonzeratu zifulumira kudza. Popeza Yehova adzaweruza anthu ake, nadzachitira nsoni anthu ake; pakuona Iye kuti mphamvu yao yatha, wosatsala womangika kapena waufulu. Pamenepo adzati, Ili kuti milungu yao, thanthwe limene anathawirako? Imene inadya mafuta a nsembe zao zophera, nimwa vinyo wa nsembe yao yothira? Iuke nikuthandizeni, Ikhale pobisalapo panu. Tapenyani tsopano kuti Ine ndine Iye, ndipo palibe mulungu koma Ine; ndipha Ine, ndikhalitsanso ndi moyo, ndikantha, ndichizanso Ine; ndipo palibe wakulanditsa m'dzanja langa. Pakuti ndikweza dzanja langa kuloza kumwamba, ndipo nditi, Pali moyo wanga kosatha, ndikanola lupanga langa lonyezimira, ndi dzanja langa likagwira chiweruzo; ndidzabwezera chilango ondiukira, ndi kulanga ondida. Mivi yanga ndiiledzeretsa nao mwazi, ndi lupanga langa lidzalusira nyama; ndi mwazi wa ophedwa ndi ogwidwa, ndi mutu wachitsitsi wa mdani. Kondwerani, amitundu inu, ndi anthu ake; adzalipsira mwazi wa atumiki ake, adzabwezera chilango akumuukira, nadzafafanizira zoipa dziko lake, ndi anthu ake. Ndipo anadza Mose nanena mau onse a nyimbo iyi m'makutu mwa anthu, iye, ndi Yoswa mwana wa Nuni. Ndipo Mose anatha kunena mau awa onse kwa Israele wonse; nati nao, Ikani mitima yanu pa mau onse ndikuchitirani nao mboni lero; kuti muuze ana anu asamalire kuwachita mau onse a chilamulo ichi. Pakuti sichikhala kwa inu chinthu chopanda pake, popeza ndicho moyo wanu, ndipo mwa chinthu ichi mudzachulukitsa masiku anu m'dziko limene muolokera Yordani, kulilandira. Ndipo Yehova ananena ndi Mose tsiku lomweli, ndi kuti, Kwera m'phiri muno mwa Abarimu, phiri la Nebo, lokhala m'dziko la Mowabu, popenyana ndi Yeriko; nupenye dziko la Kanani, limene ndipereka kwa ana a Israele likhale laolao; nufe m'phiri m'mene ukweramo, nuitanidwe kunka kwa anthu a mtundu wako; monga Aroni mbale wako anafa m'phiri la Hori, naitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wake; popeza munandilakwira pakati pa ana a Israele ku madzi a Meriba wa Kadesi m'chipululu cha Zini, popeza simunandipatula Ine pakati pa ana a Israele. Pakuti udzapenya dzikoli pandunji pako; koma osalowako ku dziko limene ndipatsa ana a Israele. Ndipo mdalitso, Mose munthu wa Mulungu anadalitsa nao ana a Israele asanafe, ndi uwu. Ndipo anati, Yehova anafuma ku Sinai, nawatulukira ku Seiri; anaoneka wowala pa phiri la Parani, anafumira kwa opatulika zikwizikwi; ku dzanja lamanja lake kudawakhalira lamulo lamoto. Inde akonda mitundu ya anthu; opatulidwa ake onse ali m'dzanja mwanu; ndipo akhala pansi ku mapazi anu; yense adzalandirako mau anu. Mose anatiuza chilamulo, cholowa cha msonkhano wa Yakobo. Ndipo Iye anali mfumu m'Yesuruni, pakusonkhana mafumu a anthu, pamodzi ndi mafuko a Israele. Rubeni akhale ndi moyo, asafe, koma amuna ake akhale owerengeka. Za Yuda ndi izi; ndipo anati, Imvani, Yehova, mau a Yuda, ndipo mumfikitse kwa anthu ake; manja ake amfikire; ndipo mukhale inu thandizo lake pa iwo akumuukira. Ndipo za Levi anati, Tumimu ndi Urimu wanu zikhala ndi wokondedwa wanu, amene mudamuyesa m'Masa, amene mudalimbana naye ku madzi a Meriba; amene anati za atate wake ndi amai wake, sindinamuone; Sanazindikire abale ake, sanadziwe ana ake omwe; popeza anasamalira mau anu, nasunga chipangano chanu. Adzaphunzitsa Yakobo maweruzo anu, ndi Israele chilamulo chanu; adzaika chofukiza pamaso panu, ndi nsembe yopsereza yamphumphu pa guwa la nsembe lanu. Dalitsani, Yehova, mphamvu yake, nimulandire ntchito ya manja ake; akantheni m'chuuno iwo akumuukira, ndi iwo akumuda, kuti asaukenso. Za Benjamini anati, Wokondedwa wa Yehova adzakhala ndi Iye mokhazikika; am'phimba tsiku lonse, inde akhalitsa pakati pa mapewa ake. Ndipo za Yosefe anati, Yehova adalitse dziko lake; ndi zinthu zofunikatu za m'mwamba, ndi mame, ndi madzi okhala pansipo; ndi zipatso zofunikatu za dzuwa, ndi zomera zofunikatu za mwezi, ndi zinthu zoposa za mapiri akale, ndi zinthu zofunikatu za zitunda zosatha, ndi zinthu zofunikatu za dziko lapansi, ndi kudzala kwake, ndi chivomerezo cha Iye anakhala m'chitsambayo. Mdalitso ufike pa mutu wa Yosefe, ndi pakati pa mutu wake wa iye wokhala padera ndi abale ake. Woyamba kubadwa wa ng'ombe yake, ulemerero ndi wake; nyanga zake ndizo nyanga zanjati; adzatunga nazo mitundu ya anthu pamodzi, kufikira malekezero a dziko lapansi. Iwo ndiwo zikwi khumi za Efuremu, iwo ndiwo zikwi za Manase. Ndi za Zebuloni anati, Kondwera, Zebuloni, ndi kutuluka kwako; ndi Isakara, m'mahema mwako. Adzaitana mitundu ya anthu afike kuphiri; apo adzaphera nsembe za chilungamo; popeza adzayamwa zochuluka za m'nyanja, ndi chuma chobisika mumchenga. Ndi za Gadi anati, Wodala iye amene akuza Gadi; akhala ngati mkango waukazi, namwetula dzanja, ndi pakati pa mutu pomwe. Ndipo anadzisankhira gawo loyamba, popeza kumeneko kudasungika gawo la wolamulira; ndipo anadza ndi mafumu a anthu, anachita chilungamo cha Yehova, ndi maweruzo ake ndi Israele. Ndi za Dani anati, Dani ndiye mwana wa mkango, wakutumpha motuluka m'Basani. Za Nafutali anati, Nafutali, wokhuta nazo zomkondweretsa, wodzala ndi mdalitso wa Yehova; landira kumadzulo ndi kumwera. Ndi za Asere anati, Asere adalitsidwe mwa anawo; akhale wovomerezeka mwa abale ake, aviike phazi lake m'mafuta. Nsapato zako zikhale za chitsulo ndi mkuwa; ndipo monga masiku ako momwemo mphamvu yako. Palibe wina ngati Mulungu, Yesuruni iwe, wakuyenda wokwera pathambo, kukuthandiza, ndi pa mitambo m'ukulu wake. Mulungu wamuyaya ndiye mokhaliramo mwako; ndi pansipo pali manja osatha. Ndipo aingitsa mdani pamaso pako, nati, Ononga. Ndipo Israele akhala mokhazikika pa yekha; kasupe wa Yakobo; akhala m'dziko la tirigu ndi vinyo; inde thambo lake likukha mame. Wodala iwe, Israele; akunga iwe ndani, mtundu wa anthu opulumutsidwa ndi Yehova, ndiye chikopa cha thandizo lako, Iye amene akhala lupanga la ukulu wako! Ndi adani ako adzakugonjera; ndipo udzaponda pa misanje yao. Ndipo Mose anakwera kuchokera ku zidikha za Mowabu, kunka kuphiri la Nebo, pamwamba pa Pisiga, popenyana ndi Yeriko. Ndipo Yehova anamuonetsa dziko lonse la Giliyadi, kufikira ku Dani; ndi Nafutali lonse, ndi dziko la Efuremu, ndi Manase, ndi dziko lonse la Yuda, kufikira nyanja ya m'tsogolo; ndi kumwera, ndi chidikha cha chigwa cha Yeriko, mudzi wa migwalangwa, kufikira ku Zowari. Ndipo Yehova anati kwa iye, Si ili dziko ndinalumbirira Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, ndi kuti, Ndidzalipereka kwa mbeu zako. Ndinakuonetsa ili m'maso, koma sudzaolokako. Ndipo Mose mtumiki wa Yehova anamwalirako m'dziko la Mowabu, monga mwa mau a Yehova. Ndipo Iye anamuika m'chigwa m'dziko la Mowabu popenyana ndi Betepeori; koma palibe munthu wakudziwa kumanda kwake kufikira lero lino. Ndipo zaka zake za Mose ndizo zana limodzi ndi makumi awiri, pakumwalira iye; diso lake silinachita mdima, ndi mphamvu yake siidaleka. Ndipo ana a Israele analira Mose m'zidikha za Mowabu masiku makumi atatu; potero anatha masiku akulira maliro a Mose. Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anadzala ndi mzimu wanzeru; popeza Mose adamuikira manja ake; ndi ana a Israele anamvera iye, nachita monga Yehova adauza Mose. Ndipo sanaukenso mneneri m'Israele ngati Mose, amene Yehova anadziwana naye popenyana maso; kunena za zizindikiro ndi zozizwa zonse zimene Yehova anamtumiza kuzichita m'dziko la Ejipito kwa Farao, ndi anyamata ake onse, ndi dziko lake lonse; ndi kunena za dzanja la mphamvu lonse, ndi choopsa chachikulu chonse, chimene Mose anachita pamaso pa Israele wonse. Ndipo atafa Mose mtumiki wa Yehova, Yehova anati kwa Yoswa mwana wa Nuni mnyamata wa Mose, Mose mtumiki wanga wafa; tauka tsono, nuoloke Yordani uyu, iwe ndi anthu awa onse, kulowa m'dzikomo ndilikuwapatsa, ndiwo ana a Israele. Pali ponse phazi lanu lidzapondapo ndinakupatsani, monga ndinanena ndi Mose. Kuyambira chipululu, ndi Lebanoni uyu, kufikira mtsinje waukulu mtsinje wa Yufurate, dziko lonse la Ahiti, ndi kufikira Nyanja Yaikulu ku malowero a dzuwa, ndiwo malire anu. Palibe munthu adzatha kuima pamaso pako masiku onse a moyo wako; monga ndinakhala ndi Mose momwemo ndidzakhala ndi iwe; sindidzakusowa, sindidzakusiya. Khala wamphamvu, nulimbike mtima, pakuti udzagawira anthu awa dzikoli likhale cholowa chao, ndilo limene ndinalumbirira makolo ao kuwapatsa. Komatu khala wamphamvu, nulimbike mtima kwambiri, kuti usamalire kuchita monga mwa chilamulo chonse anakulamuliracho Mose mtumiki wanga; usachipatukire ku dzanja lamanja kapena kulamanzere, kuti ukachite mwanzeru kulikonse umukako. Buku ili la chilamulo lisachoke pakamwa pako; koma ulingiriremo usana ndi usiku, kuti usamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwamo; popeza ukatero udzakometsa njira yako, nudzachita mwanzeru. Kodi sindinakulamulira iwe? Khala wamphamvu, nulimbike mtima, usaope, kapena kutenga nkhawa, pakuti Yehova Mulungu wako ali ndi iwe kulikonse umukako. Pamenepo Yoswa analamulira akapitao a anthu, ndi kuti, Pitani pakati pa chigono, nimulamulire anthu, ndi kuti, Mudzikonzeretu kamba, pakuti asanapite masiku atatu mudzaoloka Yordani uyu, kulowa ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, likhale lanulanu. Ndipo Yoswa anati kwa Arubeni, ndi Agadi, ndi fuko la Manase logawika pakati, ndi kuti, Kumbukirani mau amene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulirani inu, kuti, Yehova Mulungu wanu akupatsani mpumulo, nadzakupatsani dziko lino. Akazi anu, ana anu, ndi zoweta zanu zikhale m'dzikoli anakuninkhani Mose, tsidya lino la Yordani; koma inu muoloke okonzeka kunkhondo pamaso pa abale anu, ngwazi zonse, ndi kuwathandiza; mpaka Yehova atapatsa abale anu mpumulo, monga umo anakuninkhirani inu, naonso alandira dzikolo awaninkha Yehova Mulungu wanu; pamenepo mubwerere ku dziko lanulanu, ndi kukhala nalo, limene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani tsidya lino la Yordani la kum'mawa, Ndipo anamyankha Yoswa, nati, Zonse mwatilamulira tidzachita, ndipo kulikonse mutitumako tidzamuka. Monga momwe tinamvera mau onse a Mose momwemo tidzamvera inu; komatu akhale ndi inu Yehova Mulungu wanu monga anakhala ndi Mose. Aliyense wakupikisana ndi inu, osamvera mau anu mulimonse mukamlamulira, aphedwe; komatu khalani wamphamvu, nimulimbike mtima. Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, ali ku Sitimu, anatuma amuna awiri mosadziwika kukazonda, ndi kuti, Mukani, mulipenye dzikolo, ndi ku Yeriko. Ndipo anamuka nalowa m'nyumba ya mkazi wadama, dzina lake Rahabi, nagona momwemo. Ndipo wina anaiuza mfumu ya Yeriko, kuti, Taonani, usiku uno alowa muno amuna a ana a Israele, kulizonda dziko. Ndipo mfumu ya Yeriko inatuma wina kwa Rahabi, ndi kuti, Tulutsa amunawo anafika kwanu, amene analowa m'nyumba mwako; popeza anadzera kulizonda dziko lonse. Koma mkaziyo anatenga amuna awiriwo, nawabisa; natero, Inde, amunawo anandifikira; koma sindinadziwa uko afuma; ndipo m'mene akadati atseke pachipata, kutada, anatuluka amunawo; uko anamuka amunawo osakudziwa ine; muwalondole msanga, pakuti mudzawapeza. Koma adawakweretsa patsindwi, nawabisa ndi mitengo yanthamza yoyanika patsindwi. Ndipo amunawo anawalondola pa njira ya ku Yordani yonka kudooko; ndipo atatuluka akuwalondola, anatseka pachipata. Koma asanagone iwo, anawakwerera patsindwi iye, nati kwa amunawo, Ndidziwa kuti Yehova wakupatsani dzikoli, ndi kuti kuopsa kwanu kwatigwera, ndi kuti okhala m'dziko onse asungunuka pamaso panu. Popeza tidamva kuti Yehova anaphwetsa madzi a m'Nyanja Yofiira pamaso panu, muja mudatuluka m'Ejipito; ndi chija munachitira mafumu awiri a Aamori okhala tsidya la Yordani, ndiwo Sihoni ndi Ogi, amene mudawaononga konse. Ndipo titamva ichi mitima yathu inasungunuka; analibenso mtima ndi mmodzi yense, chifukwa cha inu; pakuti Yehova Mulungu wanu, ndiye Mulungu wa m'mwamba umo, ndi pa dziko lapansi. Ndipo tsopano, mundilumbiriretu kwa Yehova, popeza ndakuchitirani chifundo, kuti inunso mudzachitira chifundo a m'nyumba ya atate wanga ndi kundipatsa chizindikiro choona, kuti mudzawasunga ndi moyo atate wanga ndi mai wanga, ndi alongo anga ndi abale anga, ndi zonse ali nazo, ndi kupulumutsa miyoyo yathu kuimfa. Ndipo amunawo anati kwa iye, Moyo wathu ndiwo moyo wanu, mukapanda kuwulula chodzera ife; ndipo kudzakhala kuti, pakutipatsa ife dziko ili Yehova, tidzakuchitira chifundo ndi choonadi. Pamenepo anawatsitsa pazenera ndi chingwe; popeza nyumba yake inali pa linga la mudzi, nakhala iye palingapo. Ndipo anati kwa iwo, Mukani kuphiri, olondola angakupezeni; mubisale kumeneko masiku atatu, mpaka atabwerera olondolawo, pamenepo muyende ulendo wanu. Ndipo amunawo anati kwa iye, Sitidzachimwira lumbiro lako ili watilumbiritsali. Taona, tikadzalowa m'dzikomo ife, uzimanga chingwe ichi chofiira pazenera pamene watitsitsira; ndipo udzasonkhanitsa m'nyumbamo atate wako ndi mai wako ndi abale ako ndi a m'nyumba onse a atate wako. Ndipo kudzakhala kuti aliyense akadzatuluka pa khomo la nyumba yako kubwalo, imfa imeneyi ndi yake, tilibe kupalamula ife; koma aliyense adzakhala ndi iwe m'nyumba, likamfikira dzanja, imfa imeneyi ndi yathu. Koma ukawulula chodzera ifecho tidzamasukira lumbiro lako watilumbiritsali. Nati iye, Momwemo, monga mwa mau anu. Ndipo anawauza amuke, iwo namuka; namanga iye chingwe chofiiracho pazenera. Ndipo anayenda iwo, nafika kuphiri, nakhalako masiku atatu mpaka atabwerera olondolawo; popeza olondolawo anawafunafuna panjira ponse, osawapeza. Pamenepo amuna awiriwo anabwerera, natsika m'phirimo naoloka, nafika kwa Yoswa mwana wa Nuni, namfotokozera zonse zidawagwera. Ndipo anati kwa Yoswa, Zoonadi, Yehova wapereka dziko lonse m'manja mwathu; ndiponso nzika zonse zasungunuka pamaso pathu. Ndipo Yoswa analawirira mamawa, kuchoka ku Sitimu, nafika ku Yordani, iye ndi ana onse a Israele; nagona komweko, asanaoloke. Ndipo kunali atapita masiku atatu, akapitao anapita pakati pa chigono; nalamulira anthu, ndi kuti, Mukadzaona likasa la chipangano la Yehova Mulungu wanu, ndi ansembe Aleviwo atalisenza, pamenepo muchoke kwanu ndi kulitsata. Koma pakhale dera pakati pa inu ndi ilo, monga mikono zikwi ziwiri poliyesa; musaliyandikire, kuti mudziwe njira imene muziyendamo; popeza simunapita njirayi kufikira lero. Ndipo Yoswa ananena kwa anthu, Mudzipatule, pakuti mawa Yehova adzachita zodabwitsa pakati pa inu. Ndipo Yoswa anati kwa ansembe, Senzani likasa la chipangano, nimuoloke pamaso pa anthu. Nasenza iwo likasa la chipangano, natsogolera anthu. Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Lero lino ndidzayamba kukukuza pamaso pa Aisraele onse, kuti adziwe, kuti monga momwe ndinakhalira ndi Mose, momwemo ndidzakhala ndi iwe. Ndipo uzilamulira ansembe akunyamula likasa la chipangano, ndi kuti, Pamene mufika kumphepete kwa madzi a Yordani muziima m'Yordani. Ndipo Yoswa anati kwa ana a Israele, Idzani kuno, mumve mau a Yehova Mulungu wanu. Nati Yoswa, Ndi ichi mudzadziwa kuti Mulungu wamoyo ali pakati pa inu, ndi kuti adzapirikitsa ndithu pamaso panu Akanani, ndi Ahiti, ndi Ahivi, ndi Aperizi, ndi Agirigasi, ndi Aamori, ndi Ayebusi. Taonani, likasa la chipangano la Ambuye wa dziko lonse lapansi lioloka Yordani pamaso panu. Ndipo tsono, mudzitengere amuna khumi ndi awiri mwa mafuko a Israele, fuko limodzi mwamuna mmodzi. Ndipo kudzakhala, akaima mapazi a ansembe akusenza likasa la Yehova Ambuye wa dziko lonse, m'madzi a Yordani, adzadulidwa madziwo, ndiwo madzi ochokera kumagwero, nadzaima mulu umodzi. Ndipo kunali pochoka anthu ku mahema ao kukaoloka Yordani, ansembe anasenza likasa la chipangano pamaso pa anthu. Ndipo pamene iwo akusenza likasa anafika ku Yordani, nathibika m'mphepete mwa madzi mapazi a ansembe akusenza likasa, pakuti Yordani asefuka m'magombe ake onse, nyengo yonse ya masika, pamenepo madzi ochokera kumagwero anaima, nauka ngati mulu, kutalitu ku Adama, ndiwo mudzi wa ku mbali ya Zaretani; koma madzi akutsikira kunka ku nyanja ya chidikha, ndiyo Nyanja ya Mchere, anadulidwa konse; ndipo anthu anaoloka pandunji pa Yeriko. Ndipo ansembe akulisenza likasa la chipangano la Yehova, anaima pouma pakati pa Yordani, ndi Aisraele onse anaoloka pouma mpaka mtundu wonse unatha kuoloka Yordani. Ndipo kunali, utatha kuoloka Yordani mtundu wonse, Yehova ananena ndi Yoswa, nati, Mudzitengere mwa anthu, amuna khumi ndi awiri, fuko limodzi mwamuna mmodzi; ndipo muwalamulire iwo ndi kuti, Mudzitengere pano pakati pa Yordani, poimapo mapazi a ansembe, miyala khumi ndi iwiri, ndi kuoloka nayo, ndi kuiika m'mogona m'mene mugonamo usiku uno. Pamenepo Yoswa anaitana amuna khumi ndi awiriwo amene anawaikiratu mwa ana a Israele, fuko limodzi mwamuna mmodzi; nanena nao Yoswa, Olokani, kutsogolera likasa la Yehova Mulungu wanu pakati pa Yordani, nimudzisenzere yense mwala paphewa pake, monga mwa kuwerenga kwa mafuko a ana a Israele; kuti ichi chikhale chizindikiro pakati pa inu. Akakufunsani ana anu m'tsogolomo, ndi kuti, Miyala iyi nja chiyani ndi inu? Munene nao, Chifukwa madzi a Yordani anadulidwa patsogolo pa likasa la chipangano cha Yehova; muja lidaoloka Yordani, madzi a Yordani anadulidwa; ndipo miyala iyi idzakhala chikumbutso cha ana a Israele chikhalire. Ndipo ana a Israele anachita monga Yoswa anawalamulira, nasenza miyala khumi ndi iwiri pakati pa Yordani, monga Yehova adalankhula ndi Yoswa, monga mwa kuwerenga kwa mafuko a ana a Israele; ndipo anaoloka nayo kunka kogona, naiika komweko. Ndipo Yoswa anaimika miyala khumi ndi iwiri pakati pa Yordani, poimapo mapazi a ansembe akusenza likasa la chipangano; ikhala komweko kufikira lero lino. Pakuti ansembe akusenza likasa anaima pakati pa Yordani, mpaka zitatha zonse Yehova adazilamulira Yoswa anene kwa anthu, monga mwa zonse Mose adalamulira Yoswa; ndipo anthu anafulumira kuoloka. Ndipo kunali, atatha kuoloka anthu onse, likasa la Yehova linaoloka, ndi ansembe, pamaso pa anthu. Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi gawo lija la fuko la Manase anaoloka ndi zida zao pamaso pa ana a Israele, monga Mose adanena nao; ngati zikwi makumi anai ankhondo okonzeka anaoloka pamaso pa Yehova kuthira nkhondo ku zidikha za Yeriko. Tsiku lomwelo Yehova anakulitsa Yoswa pamaso pa Aisraele onse; ndipo anamuopa monga anaopa Mose, masiku onse a moyo wake. Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Lamulira ansembe akusenza likasa la umboni, kuti akwere kutuluka m'Yordani. Pamenepo Yoswa analamulira ansembe, ndi kuti, Kwerani kutuluka m'Yordani. Ndipo kunali, atakwera ansembe akusenza likasa la chipangano la Yehova, kutuluka pakati pa Yordani, nakwera pamtunda mapazi a ansembe, madzi a m'Yordani anabwera m'njira mwake, nasefuka m'magombe ake onse monga kale. Ndipo anthu anakwera kutuluka m'Yordani tsiku lakhumi la mwezi woyamba, namanga misasa ku Giligala, mbali ya ku m'mawa kwa Yeriko. Ndipo Yoswa anaimika ku Giligala miyala ija khumi ndi iwiri adaitenga m'Yordani. Ndipo anati kwa ana a Israele, Ana anu akadzafunsa atate ao masiku akudza, ndi kuti, Miyala iyi nja chiyani? Pamenepo muzidziwitsa ana anu, ndi kuti, Israele anaoloka Yordani uyu pouma. Pakuti Yehova Mulungu wanu anaphwetsa madzi a Yordani pamaso panu, mpaka mutaoloka; monga Yehova Mulungu wanu anachitira Nyanja Yofiira, imene anaiphwetsa pamaso pathu, mpaka titaoloka; kuti mitundu yonse ya pa dziko lapansi idziwe dzanja la Yehova, kuti ndilo lamphamvu; kuti iope Yehova Mulungu wanu masiku onse. Ndipo kunali, pamene mafumu onse a Aamori okhala tsidya la kumadzulo la Yordani, ndi mafumu onse a Akanani okhala ku nyanja anamva kuti Yehova anaphwetsa madzi a Yordani pamaso pa ana a Israele mpaka titaoloka, mtima wao unasungunuka, analibenso moyo chifukwa cha ana a Israele. Nthawi imeneyo Yehova anati kwa Yoswa, Udzisemere mipeni yamiyala nudulenso ana a Israele kachiwiri. Ndipo Yoswa anadzisemera mipeni yamiyala nadula ana a Israele pa Gibea-Naraloti. Koma chifukwa chakuti Yoswa anawadula ndi ichi: anthu onse otuluka m'Ejipito, anthu amuna, ndiwo amuna onse ankhondo, adafa m'chipululu panjira, atatuluka m'Ejipito. Pakuti anthu onse anatulukawo anadulidwa; koma anthu onse obadwa m'chipululu panjira potuluka m'Ejipito sanadulidwe. Pakuti ana a Israele anayenda m'chipululu zaka makumi anai, mpaka mtundu wonse wa amuna ankhondo otuluka m'Ejipito udatha, chifukwa cha kusamvera mau a Yehova; ndiwo amene Yehova anawalumbirira kuti sadzawaonetsa dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kudzatipatsa, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi. Koma ana ao amuna amene anawautsa m'malo mwao, iwowa Yoswa anawadula; popeza anakhala osadulidwa, pakuti sanawadule panjira. Ndipo kunali, atatha kudula mtundu wonse, anakhala m'malo mwao m'chigono mpaka adachira. Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Lero lino ndakukunkhunizirani mtonzo wa Ejipito. Chifukwa chake dzina la malowo analitcha Giligala kufikira lero lino. Ndipo ana a Israele anamanga misasa ku Giligala; nachita Paska tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi, madzulo, m'zidikha za Yeriko. Ndipo m'mawa mwake atatha Paska, anadya tirigu wakhwimbi wa m'dziko, mikate yopanda chotupitsa ndi tirigu wokazinga tsiku lomwe lija. Koma m'mawa mwake mana analeka, atadya iwo tirigu wakhwimbi wa m'dziko; ndipo ana a Israele analibenso mana; koma anadya zipatso za dziko la Kanani chaka chomwe chija. Ndipo kunali, pokhala Yoswa ku Yeriko, anakweza maso ake, napenya, ndipo taona, panaima munthu pandunji pake ndi lupanga lake losolola m'dzanja lake; namuka Yoswa kuli iye, nati iye, Uvomerezana ndi ife kapena ndi adani athu? Nati, Iai, koma ndadza ine, kazembe wa ankhondo a Yehova. Pamenepo Yoswa anagwa nkhope yake pansi, napembedza, nati kwa iye, Anenanji Ambuyanga kwa mtumiki wake? Ndipo kazembe wa ankhondo a Yehova anati kwa Yoswa, Vula nsapato yako pa phazi lako; pakuti malo upondapo mpopatulika. Nachita Yoswa chomwecho. Koma ku Yeriko anatseka pazipata, natsekedwa chifukwa cha ana a Israele, panalibe wotuluka, panalibenso wolowa. Ndipo Yehova ananena kwa Yoswa, Taona, ndapereka m'dzanja lako Yeriko ndi mfumu yake, ndi ngwazi zake. Ndipo muzizungulira mudzi inu nonse ankhondo, kuuzungulira mudzi kamodzi. Muzitero masiku asanu ndi limodzi. Ndipo ansembe asanu ndi awiri azinyamula mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo, natsogolere nazo likasa; koma tsiku lachisanu ndi chiwiri mudzizungulira mudziwo kasanu ndi kawiri, ndi ansembe aziliza mphalasazo. Ndipo kudzakhala kuti akaliza chilizire ndi nyanga ya nkhosa yamphongo, nimumva kulira kwa mphalasa, anthu onse afuule mfuu yaikulu; ndipo linga la mudziwo lidzagwa pomwepo, ndi anthu adzakwera ndi kulowamo yense kumaso kwake. Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anaitana ansembe, nanena nao, Senzani likasa la chipangano, ndi ansembe asanu ndi awiri anyamule mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo, kutsogolera nazo likasa la Yehova. Nati kwa anthu, Pitani, muzizungulira mudzi, ndi ankhondo ndi zida zao atsogolere likasa la Yehova. Ndipo atanena kwa anthu Yoswa, ansembe asanu ndi awiri akunyamula mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo pamaso pa Yehova, anapita naliza mphalasazo; ndipo likasa la chipangano cha Yehova linawatsata. Ndipo okonzeka kunkhondo anatsogolera ansembe akuliza mphalasa, koma akudza m'mbuyo anatsata likasa, ansembe ali chiombere poyenda iwo. Ndipo Yoswa analamulira anthu, ndi kuti, Musamafuula, kapena kumveketsa mau anu, asatuluke konse mau m'kamwa mwanu, mpaka tsiku lakunena nanu ine, Fuulani; pamenepo muzifuula. Ndipo anazungulitsa likasa la Yehova mudzi, kuzungulira kamodzi; pamenepo analowa kuchigono, nagona m'mwemo. Ndipo Yoswa analawira mamawa, ndi ansembe anasenza likasa la Yehova. Ndipo ansembe asanu ndi awiri, akunyamula mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo ndi kutsogolera nazo likasa la Yehova, anayenda chiyendere naliza mphalasazo; ndi okonzeka kunkhondowo anawatsogolera, ndi akudza m'mbuyo anatsata likasa la Yehova, ansembe ali chiombere poyenda iwo. Ndipo tsiku lachiwiri anazungulira mudzi kamodzi, nabwera kuchigono; anatero masiku asanu ndi limodzi. Ndipo kunali, tsiku lachisanu ndi chiwiri analawira mamawa, mbandakucha, nazungulira mudzi mommuja kasanu ndi kawiri; koma tsiku lijalo anazungulira mudzi kasanu ndi kawiri. Ndipo kunali, pa nthawi yachisanu ndi chiwiri, pamene ansembe analiza mphalasa, Yoswa anati kwa anthu, Fuulani; pakuti Yehova wakupatsani mudziwo. Koma mudziwo udzaperekedwa kwa Yehova ndi kuonongeka konse, uwu ndi zonse zili m'mwemo; Rahabi yekha wadamayo adzakhala ndi moyo, iye ndi onse ali naye m'nyumba, chifukwa anabisa mithenga tinawatumawo. Ndipo inu, musakhudze choperekedwacho, mungadziononge konse, potapa choperekedwacho; ndi kuononga konse chigono cha Israele ndi kuchisautsa. Koma siliva yense, ndi golide yense, ndi zotengera za mkuwa ndi chitsulo zikhala chopatulikira Yehova; zilowe m'mosungira chuma cha Yehova. Ndipo anthu anafuula, naliza mphalasa ansembe; ndipo kunali, pamene anthu anamva kulira kwa mphalasa, anafuula anthu ndi mfuu yaikulu, niligwa linga pomwepo; nakwera anthu kulowa m'mudzi, yense kumaso kwake; nalanda mudziwo. Ndipo anapereka kuziononga ndi lupanga lakuthwa zonse za m'mudzi, amuna ndi akazi omwe, ana ndi nkhalamba zomwe, kudza ng'ombe, ndi nkhosa, ndi abulu, ndi lupanga lakuthwa. Ndipo Yoswa ananena kwa amuna awiri anazonda dzikowo, Lowani m'nyumba ya mkazi wadamayo, ndi kutulutsamo mkaziyo ndi zonse ali nazo, monga munamlumbirira iye. Pamenepo anyamata ozondawo analowa, natulutsa Rahabi, ndi atate wake ndi mai wake ndi abale ake, ndi onse anali nao; anatulutsanso achibale ake onse; nawaika kunja kwa chigono cha Israele. Ndipo anatentha mudzi ndi moto, ndi zonse zinali m'mwemo; koma siliva ndi golide ndi zotengera zamkuwa ndi zachitsulo anaziika m'mosungira chuma cha nyumba ya Yehova. Koma Rahabi, mkazi wadamayo ndi banja la atate wake, ndi onse anali nao, Yoswa anawasunga ndi moyo; ndipo anakhala pakati pa Israele mpaka lero lino; chifukwa anabisa mithenga imene Yoswa anaituma kuzonda Yeriko. Ndipo Yoswa anawalumbirira nyengo ija, ndi kuti, Wotembereredwa pamaso pa Yehova munthu amene adzauka ndi kumanga mudzi uwu wa Yeriko; adzamanga kuzika kwake ndi kutayapo mwana wake woyamba, nadzaimika zitseko zake ndi kutayapo mwana wake wotsirizira. Potero Yehova anakhala ndi Yoswa; ndi mbiri yake inabuka m'dziko lonse. Koma ana a Israele analakwa ndi choperekedwacho; popeza Akani mwana wa Karimi, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda, anatapa choperekedwacho; ndi mkwiyo wa Yehova unayakira ana a Israele. Ndipo Yoswa anatuma amuna kuchokera ku Yeriko apite ku Ai, ndiwo pafupi pa Betaveni, kum'mawa kwa Betele; nanena nao, Kwerani ndi kukazonda dziko. Nakwera amunawo, nazonda Ai. Ndipo anabwera kwa Yoswa, nati kwa iye, Asakwere anthu onse; koma akwere amuna ngati zikwi ziwiri kapena zitatu kukantha Ai; musalemetsa anthu onse kumkako, pakuti a komweko ndi owerengeka. Potero mwa anthu anakwerako amuna monga zikwi zitatu; koma anathawa pamaso pa amuna a ku Ai. Ndipo amuna a ku Ai anawakantha amuna, ngati makumi atatu mphambu asanu ndi mmodzi; nawapirikitsa kuyambira pachipata mpaka ku Sebarimu, nawakantha potsika; ndi mitima ya anthu inasungunuka inga madzi. Ndipo Yoswa anang'amba zovala zake, nagwa nkhope yake pansi, ku likasa la Yehova, mpaka madzulo, iye ndi akuluakulu a Israele, nathira fumbi pamitu pao. Ndipo Yoswa anati, Ha! Ambuye, Yehova, mwaolotseranji anthu awa pa Yordani, kutipereka ife m'dzanja la Aamori, kutiononga ife? Mwenzi titalola ndi kukhala tsidya lija la Yordani! Ndidzanenanji, Ambuye, Israele atabwerera m'mbuyo pamaso pa adani ao? Akadzamva ichi Akanani ndi okhala m'dziko onse, adzatizinga ndi kuduliratu dzina lathu pa dziko lapansi; ndipo mudzachitiranji dzina lanu lalikulu? Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Tauka, wagweranji pankhope pako chotere? Israele wachimwa, nalakwiranso chipangano changa, ndinawalamuliracho; natengakonso choperekedwacho; anabanso, nanyenganso, nachiika pakati pa akatundu ao. Mwa ichi ana a Israele sangathe kuima pamaso pa adani ao, awafulatira adani ao, pakuti aperekedwa aonongeke. Sindidzakhalanso nanu mukapanda kuononga choperekedwacho, kuchichotsa pakati pa inu. Tauka, patula anthu, nuti, Mudzipatulire mawa; pakuti atero Yehova Mulungu wa Israele, Pali choperekedwa chionongeke pakati pako, Israele iwe; sukhoza kuima pamaso pa adani ako, mpaka mutachotsa choperekedwacho pakati panu. Koma m'mawa adzakuyandikitsani, fuko ndi fuko; ndipo kudzali kuti fukoli Yehova aliwulula lidzayandikira mwa zibale zake; ndi chibale Yehova achiwulula chidzayandikira monga mwa a nyumba ake; ndi a m'nyumbawo Yehova awawulula adzayandikira mmodzimmodzi. Ndipo kudzali kuti iye wogwidwa ali nacho choperekedwacho adzatenthedwa ndi moto, iye ndi zonse ali nazo chifukwa analakwira chipangano cha Yehova, ndi chifukwa anachita chopusa m'Israele. Ndipo Yoswa analawira mamawa, nayandikizitsa Israele, fuko ndi fuko; ndi fuko la Yuda linagwidwa; nayandikizitsa zibale za Yuda, nagwira chibale cha Azera; nayandikizitsa chibale cha Azera, mmodzimmodzi, nagwidwa Zabidi; nayandikizitsa a m'nyumba yake mmodzimmodzi; ndipo Akani, mwana wa Karimi, mwanu wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda anagwidwa. Ndipo Yoswa anati kwa Akani, Mwana wanga, uchitiretu ulemu Yehova Mulungu wa Israele, numlemekeze Iye; nundiuze tsopano, wachitanji? Usandibisire. Ndipo Akani anayankha Yoswa nati, Zoonadi, ndachimwira Yehova Mulungu wa Israele, ndachita zakutizakuti; pamene ndinaona pazofunkha malaya abwino a ku Babiloni, ndi masekeli mazana awiri a siliva, ndi chikute chagolide, kulemera kwake masekeli makumi asanu, ndinazikhumbira ndi kuzitenga; ndipo taonani, ndazibisa m'nthaka pakati pa hema wanga, ndi siliva pansi pakepo. Pamenepo Yoswa anatuma mithenga, iwo nathamangira kuhema; ndipo taonani, zidabisika m'hema mwake ndi siliva pansi pake. Ndipo anazichotsa pakati pa hema, nabwera nazo kwa Yoswa ndi kwa ana onse a Israele, nazitula pamaso pa Yehova. Ndipo Yoswa, ndi Aisraele onse naye, anatenga Akani mwana wa Zera, ndi siliva, ndi malayawo, ndi chikute chagolide, ndi ana ake aamuna ndi aakazi, ndi ng'ombe zake, ndi abulu ake, ndi nkhosa zake, ndi hema wake ndi zake zonse; nakwera nazo ku chigwa cha Akori. Ndipo Yoswa anati, Watisautsiranji? Yehova adzakusautsa lero lino. Ndipo Aisraele onse anamponya miyala, nawatentha ndi moto, nawaponya miyala. Ndipo anamuunjikira mulu waukulu wamiyala, wokhalako kufikira lero lino; ndipo Yehova anatembenuka kusiya mkwiyo wake waukulu. Chifukwa chake anatcha dzina lake la malowo, Chigwa cha Akori, mpaka lero lino. Pamenepo Yehova anati kwa Yoswa, Usaope, kapena kutenga nkhawa, tenga anthu onse a nkhondo apite nawe, ndipo tauka, kwera ku Ai; taona, ndapereka m'dzanja lako mfumu ya ku Ai, ndi anthu ake ndi mudzi wake ndi dziko lake; ndipo uzimchitira Ai ndi mfumu yake monga umo unamchitira Yeriko ndi mfumu yake; koma zofunkha zake ndi ng'ombe zake mudzifunkhire nokha; udziikire anthu alalire kukhonde kwa mudzi. Pamenepo anauka Yoswa, ndi anthu onse a nkhondo, kuti akwere ku Ai; ndipo Yoswa anasankha amuna zikwi makumi atatu, ndiwo ngwazi, nawatumiza apite usiku, nawalamulira ndi kuti, Taonani, muzikhala olalira kukhonde kwa mudzi; musakhalira kutali ndi mudzi, koma mukhale okonzekeratu nonse; ndipo ine, ndi anthu onse ali nane, tidzayandikira mudzi; ndipo kudzali, pamene atuluka kudzakomana nafe, monga poyamba paja, tidzathawa pamaso pao; ndipo adzatuluka kutitsata mpaka tidawakokera asiyane ndi mudzi; pakuti adzanena, Atithawa pamaso pathu monga poyamba paja; nafenso tidzathawa pamaso pao; pamenepo muziuka m'molalira ndi kulowa m'mudzi; pakuti Yehova Mulungu wanu; adzaupereka m'manja mwanu. Ndipo kudzali, mutagwira mudzi, muzitentha mudziwo ndi moto; muzichita monga mwa mau a Yehova; taonani, ndakulamulirani. Ndipo Yoswa anawatuma, namuka iwo kulowa m'molalira, nakhala pakati pa Betele ndi Ai, kumadzulo kwa Ai; koma Yoswa anakhala mwa anthu usiku uja. Ndipo Yoswa analawira m'mamawa, nayesa anthu, nakwera, iye ndi akulu a Israele, pamaso pa anthu a ku Ai. Ndi anthu onse a nkhondo okhala naye anakwera, nayandikira nafika pamaso pa mudzi, namanga misasa kumpoto kwa Ai; koma pakati pa iye ndi Ai panali chigwa. Ndipo anatenga amuna ngati zikwi zisanu, nawaika m'molalira pakati pa Betele ndi Ai, kumadzulo kwa mudzi. Momwemo anaika anthu, khamu lonse lokhala kumpoto kwa mudzi, ndi olalira ao kumadzulo kwa mudzi, ndipo usiku uja Yoswa analowa pakati pa chigwa. Ndipo kunali, pamene mfumu ya ku Ai anachiona, anafulumira iwo, nalawira mamawa, natuluka amuna a m'mudzi kuthirana ndi Israele, iye ndi anthu ake onse, poikidwiratu patsogolo pa chidikha; popeza sanadziwe kuti amlalira kukhonde kwa mudzi. Ndipo Yoswa ndi Aisraele onse anaoneka ngati a ku Ai alikuwathyola, nathawira njira ya kuchipululu. Pamenepo anthu onse okhala m'mudzi, anaitanidwa awapirikitse, nampirikitsa Yoswa, nakokedwa kusiyana ndi mudzi. Ndipo sanatsale mwamuna mmodzi yense m'Ai kapena m'Betele osatulukira kwa Israele; nasiya mudzi wapululu, napirikitsa Israele. Pamenepo Yehova anati kwa Yoswa, Tambasula nthungoyo ili m'dzanja lako iloze ku Ai, pakuti ndidzaupereka m'dzanja lako. Ndipo Yoswa anatambasula nthungoyo inali m'dzanja lake kuloza mudzi. Nauka msanga olalirawo m'mbuto mwao, nathamanga pamene anatambasula dzanja lake, nalowa m'mudzi, naugwira; nafulumira nayatsa mudziwo. Pamene amuna a ku Ai anacheuka, anapenya, ndipo taonani, utsi wa mudzi unakwera kumwamba; nasowa mphamvu iwo kuthawa chakuno kapena chauko; ndi anthu othawira kuchipululu anatembenukira owapirikitsa. Ndipo pakupenya Yoswa ndi Israele yense kuti olalirawo adagwira mudzi, ndi kuti utsi wa mudzi unakwera, anabwerera, nawapha amuna a ku Ai. A kumudzinso anawatulukira; potero anakhala pakati pa Israele, ena mbali ina, ena mbali ina; ndipo anawakantha, mpaka sanatsale kapena kupulumuka wa iwo ndi mmodzi yense. Koma mfumu ya ku Ai anamgwira wamoyo, nadza naye kwa Yoswa. Ndipo kunali, atatha Israele kupha nzika zonse za ku Ai, kuthengo, kuchipululu kumene anawapirikitsira, natha onse kugwa ndi lupanga lakuthwa mpaka adathedwa onse, Aisraele onse anabwerera ku Ai, naukantha ndi lupanga lakuthwa. Ndipo onse amene adagwa tsiku lija, amuna ndi akazi, ndiwo zikwi khumi ndi ziwiri, anthu onse a ku Ai. Popeza Yoswa sanabweze dzanja lake limene anatambasula nalo nthungo, mpaka ataononga konse nzika zonse za ku Ai. Koma ng'ombe ndi zofunkha za mudzi uwu Israele anadzifunkhira monga mwa mau a Yehova amene analamulira Yoswa. Ndipo Yoswa anatentha Ai, nausandutsa muunda ku nthawi yonse, bwinja kufikira lero lino. Ndipo mfumu ya ku Ai, anampachika pamtengo mpaka madzulo; koma polowa dzuwa Yoswa analamulira kuti atsitse mtembo wake pamtengo; ndipo anauponya polowera pa chipata cha mudzi; naunjikako mulu waukulu wamiyala, mpaka lero lino. Pomwepo Yoswa anamangira Yehova Mulungu wa Israele guwa la nsembe m'phiri la Ebala, monga Mose mtumiki wa Mulungu adalamulira ana a Israele, monga mulembedwa m'buku la chilamulo cha Mose, guwa la nsembe la miyala yosasema, yoti palibe munthu anakwezapo chitsulo; ndipo anafukizirapo Yehova nsembe zopsereza, naphera nsembe zoyamika. Ndipo analembapo pa miyalayi chitsanzo cha chilamulo cha Mose, chimene analembera pamaso pa ana a Israele. Ndipo Aisraele onse, ndi akulu ao, ndi akapitao ao, ndi oweruza ao anaima chakuno ndi chauko cha likasa, pamaso pa ansembe Alevi, akusenza likasa la chipangano la Yehova, mbadwa ndi alendo omwe; ena a iwo pandunji pa phiri la Gerizimu, ndi ena pandunji pa phiri la Ebala; monga Mose, mtumiki wa Yehova, adalamulira poyamba paja kuti adalitse anthu a Israele. Atatero, anawerenga mau onse a chilamulo, dalitso ndi temberero, monga mwa zonse zolembedwa m'buku la chilamulo. Panalibe mau amodzi a zonse adazilamulira Mose osawerenga Yoswa pamaso pa msonkhano wonse wa Israele, ndi akazi ndi ang'ono, ndi alendo akuyenda pakati pao. Ndipo kunali, pakumva ichi mafumu onse a tsidya ilo la Yordani, kumapiri ndi kuchidikha, ndi ku madooko onse a Nyanja Yaikulu, pandunji pa Lebanoni: Ahiti ndi Aamori, Akanani, Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi; anasonkhana kuponyana ndi Yoswa ndi Israele, ndi mtima umodzi. Koma pamene nzika za Gibiyoni zinamva zimene Yoswa adachitira Yeriko ndi Ai, zinachita momchenjerera, nizimuka nizioneka ngati mithenga, nizitenga matumba akale pa abulu ao, ndi matumba a vinyo akale ndi ong'ambika ndi omangamanga; ndi nsapato zakale za zigamba pa mapazi ao, nizivala nsanza; ndi mikate yonse ya kamba wao inali youma ndi yoyanga nkhungu. Ndipo zinamuka kwa Yoswa kumisasa ku Giligala, niziti kwa iye ndi kwa amuna a Israele, Tachokera dziko lakutali, chifukwa chake mupangane nafe. Ndipo amuna a Israele anati kwa Ahivi, Kapena mulimkukhala pakati pa ife, ndipo tipanganenji ndi inu? Koma anati kwa Yoswa, Ndife akapolo anu. Pamenepo Yoswa anati kwa iwo, Ndinu ayani? Ndipo mufuma kuti? Ndipo anati kwa iye, Akapolo anu afumira dziko la kutalitali, chifukwa cha dzina la Yehova Mulungu wanu; pakuti tidamva mbiri yake, ndi zonse anachita m'Ejipito, ndi zonse anachitira mafumu awiri a Aamori okhala tsidya lija la Yordani, Sihoni mfumu ya ku Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya ku Basani wokhala ku Asitaroti. Ndipo akulu athu ndi nzika zonse za m'dziko mwathu zidanena nafe ndi kuti, Mutenge m'dzanja lanu kamba wa paulendo, kakomane naoni, nimunene nao, Ndife akapolo anu; ndipo tsopano mupangane nafe. Mkate wathu uwu tinadzitengera kamba m'nyumba zathu, ukali wamoto, tsiku lotuluka ife kudza kwanu kuno; koma tsopano, taonani uli wouma ndi woyanga nkhungu; ndi matumba a vinyo awa tinawadzaza akali atsopano; ndipo taonani, ang'ambika; ndi malaya athu awa ndi nsapato zathu zatha, chifukwa cha ulendo wochokera kutali ndithu. Pamenepo amunawo analandirako kamba wao, osafunsira pakamwa pa Yehova. Ndipo Yoswa anachitirana nao mtendere napangana nao, akhale amoyo; ndi akalonga a msonkhano anawalumbirira. Ndipo kunali, atatha kupangana nao masiku atatu, anamva kuti ndiwo anansi ao, ndi kuti kwao ndi pakati pao. Ndipo ana a Israele anayenda ulendo, nafika kumidzi yao tsiku lachitatu. Koma midzi yao ndiyo Gibiyoni, ndi Kefira, ndi Beeroti ndi Kiriyati-Yearimu. Ndipo ana a Israele sanawakanthe, pakuti akalonga a msonkhano adawalumbirira kwa Yehova, Mulungu wa Israele. Ndipo msonkhano wonse unadandaula pa akalonga. Koma akalonga onse ananena kwa msonkhano wonse, Tinawalumbirira kwa Yehova Mulungu wa Israele, m'mwemo sitikhoza kuwachitira kanthu. Tidzawachitira ichi, ndi kuwasunga amoyo; ungatigwere mkwiyo chifukwa cha lumbirolo tidawalumbirira. Ndipo akalonga ananena nao, Akhale ndi moyo; ndipo anasanduka akutema nkhuni, ndi otungira madzi msonkhano wonse; monga akalonga adanena nao. Ndipo Yoswa anawaitana, nanena nao, kuti, Mwatinyenga chifukwa ninji, ndi kuti, Tikhala kutalitali ndi inu, pokhala kwanu kuli pakati pa ife? Ndipo tsopano mukhale otembereredwa, palibe mmodzi wa inu adzamasuka wosakhala kapolo, ndi kutemera nkhuni, ndi kutungira madzi nyumba ya Mulungu wanga. Ndipo anamyankha Yoswa nati, Popeza anatiuzitsa akapolo anu kuti Yehova Mulungu wanu analamulira mtumiki wake Mose kukupatsani dziko lonseli, ndi kupasula nzika zonse za m'dziko pamaso panu; potero tinaopera kwambiri moyo wathu pamaso panu, ndipo tinachita chinthuchi. Ndipo tsopano, taonani, tili m'dzanja lanu; monga muyesa chokoma ndi choyenera kutichitira ife, chitani. Pamenepo anawachitira chotero, nawalanditsa m'dzanja la ana a Israele, angawaphe. Ndipo tsiku lija Yoswa anawasandutsa akutema nkhuni, ndi otungira madzi msonkhanowo, ndi guwa la nsembe la Yehova, mpaka lero lino, pamalopo akadzasankha. Ndipo kunali, pamene Adoni-Zedeki mfumu ya Yerusalemu anamva kuti Yoswa adalanda Ai, ndi kumuononga konse; nachitira Ai ndi mfumu yake monga adachitira Yeriko ndi mfumu yake; ndi kuti nzika za Gibiyoni zinachitirana mtendere ndi Israele, nizikhala pakati pao; anaopa kwambiri, popeza Gibiyoni ndi mudzi waukulu, monga wina wa midzi yachifumu, popezanso unaposa Ai kukula kwake, ndi amuna ake onse ndiwo amphamvu. Chifukwa chake Adoni-Zedeki mfumu ya Yerusalemu anatuma kwa Hohamu, mfumu ya Hebroni, ndi kwa Piramu mfumu ya Yaramuti, ndi kwa Yafiya mfumu ya Lakisi, ndi kwa Debiri mfumu ya Egiloni, ndi kuti, Kwerani kwanga kuno, ndi kundithandiza kuti tikanthe Gibiyoni, pakuti unachitirana mtendere ndi Yoswa ndi ana a Israele. Pamenepo mafumu asanu a Aamori, ndiwo mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yaramuti, mfumu ya ku Lakisi, mfumu ya ku Egiloni anasonkhana, nakwera iwo ndi makamu ao onse namanga misasa pa Gibiyoni, nauthira nkhondo. Ndipo amuna a ku Gibiyoni anatumira Yoswa mau kuchigono ku Giligala, ndi kuti, Musalekerere akapolo anu; mutikwerere msanga, ndi kutipulumutsa, ndi kutithandiza; pakuti mafumu onse a Aamori, akukhala kumapiri atisonkhanira. Pamenepo Yoswa anakwera kuchokera ku Giligala, iye ndi anthu onse a nkhondo pamodzi naye, ndi ngwazi zonse. Ndipo Yehova ananena ndi Yoswa, Usawaope, pakuti ndawapereka m'dzanja lako; palibe mmodzi wa iwo adzaima pamaso pako. Ndipo Yoswa anawadzidzimukitsa; popeza anakwera kuchokera ku Giligala usiku wonse. Ndipo Yehova anawamwaza pamaso pa Israele, ndipo anawakantha makanthidwe akulu ku Gibiyoni, nawapirikitsa pa njira yokwera pa Betehoroni, nawakantha mpaka Azeka, ndi mpaka Makeda. Ndipo kunali, pakuthawa iwo pamaso pa Israele, potsikira pa Betehoroni, Yehova anawagwetsera miyala yaikulu yochokera kumwamba mpaka pa Azeka, nafa iwo; akufa ndi miyala yamatalala anachuluka ndi iwo amene ana a Israele anawapha ndi lupanga. Pomwepo Yoswa ananena kwa Yehova tsiku limene Yehova anapereka Aamori pamaso pa ana a Israele; ndipo anati pamaso pa Israele, Dzuwa iwe, linda, pa Gibiyoni, ndi Mwezi iwe, m'chigwa cha Ayaloni. Ndipo dzuwa linalinda, ndi mwezi unaima mpaka anthu adabwezera chilango adani ao. Kodi ichi sichilembedwa m'buku la Yasara? Ndipo dzuwa linakhala pakati pa thambo, losafulumira kulowa ngati tsiku lamphumphu. Ndipo panalibe tsiku lotere kale lonse kapena m'tsogolomo, lakuti Yehova anamvera mau a munthu; pakuti Yehova anathirira Israele nkhondo. Pamenepo Yoswa anabwezera, ndi Aisraele onse pamodzi naye, ku chigono cha ku Giligala. Ndipo mafumu awa asanu anathawa, nabisala m'phanga la ku Makeda. Ndipo anauza Yoswa ndi kuti, Mafumu asanuwa apezeka obisala m'phanga la ku Makeda. Ndipo Yoswa anati, Kunkhunizirani miyala yaikulu kukamwa kwa phanga, ndi kuikapo anthu, awasunge; koma inu musaime, pirikitsani adani anu, ndi kukantha a m'mbuyo mwao; musawalole alowe m'midzi mwao; pakuti Yehova Mulungu wanu anawapereka m'dzanja lanu. Ndipo kunali, Yoswa ndi ana a Israele atatha kuwakantha, makanthidwe akulukulu mpaka atatha psiti, ndipo otsala a iwo atalowa m'midzi ya malinga, anthu onse anabwerera kuchigono kwa Yoswa pa Makeda ndi mtendere. Palibe munthu anachitira chipongwe mmodzi yense wa ana a Israele. Pamenepo Yoswa anati, Tsegula pakamwa pa phanga ndi kunditulutsira m'phanga mafumu asanuwo. Ndipo anatero, natulutsira m'phanga mafumu asanuwo, mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yaramuti, mfumu ya ku Lakisi, mfumu ya ku Egiloni. Ndipo kunali, atatulutsira Yoswa mafumu awa, Yoswa anaitana amuna onse a Israele, ndipo anati kwa akazembe a anthu a nkhondo amene anamuka naye, Yandikirani, pondani pa makosi a mafumu awa. Nayandikira iwo, naponda pa makosi ao. Pamenepo Yoswa ananena nao, Musaope, musatenge nkhawa; khalani amphamvu, nimulimbike mtima; pakuti Yehova adzatero ndi adani anu onse amene mugwirana nao nkhondo. Ndipo atatero, Yoswa anawakantha nawapha, nawapachika pa mitengo isanu; nalikupachikidwa pa mitengo mpaka madzulo. Ndipo kunali, nthawi yakulowa dzuwa, Yoswa analamulira kuti awatsitse kumitengo; ndipo anawataya m'phanga m'mene adabisala; naika miyala yaikulu pakamwa pa phanga, mpaka lero lomwe lino. Ndipo Yoswa anagwira Makeda tsiku lomwe lija ndi kuukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi mfumu yake yomwe; anawaononga konse, ndi amoyo onse anali m'mwemo, osasiyapo ndi mmodzi yense, nachitira mfumu ya ku Makeda monga anachitira mfumu ya ku Yeriko. Pamenepo Yoswa ndi Aisraele onse naye anapitirira kuchokera ku Makeda kunka ku Libina, nathira nkhondo pa Libina; ndipo Yehova anapereka uwunso, ndi mfumu yake m'dzanja la Israele; ndipo anaukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi amoyo onse anali m'mwemo, osasiyamo ndi mmodzi yense; namchitira mfumu yake monga anachitira mfumu ya ku Yeriko. Ndipo Yoswa, ndi Aisraele onse naye, anapitirira kuchokera ku Libina kunka ku Lakisi; namanga misasa, nathira nkhondo pa uwo; napereka Yehova Lakisi m'dzanja la Israele, ndipo anaulanda tsiku lachiwiri, naukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi amoyo onse anali m'mwemo monga mwa zonse anachitira Libina. Pamenepo Horamu mfumu ya Gezere anakwera kudzathandiza Lakisi; ndipo Yoswa anamkantha iye ndi anthu ake mpaka sanamsiyire ndi mmodzi yense. Ndipo Yoswa, ndi Aisraele onse naye, anapitirira kuchokera ku Lakisi mpaka ku Egiloni; namanga misasa, nathira nkhondo. Naulanda tsiku lomwelo, naukantha ndi lupanga lakuthwa, nawaononga konse amoyo onse anali m'mwemo tsiku lomwelo, monga mwa zonse anachitira Lakisi. Ndipo Yoswa ndi Aisraele onse naye anakwera kuchokera ku Egiloni mpaka ku Hebroni, nauthira nkhondo; naulanda, naukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi mfumu yake ndi midzi yake yonse, ndi amoyo onse anali m'mwemo, osasiyapo ndi mmodzi yense, monga mwa zonse anachitira Egiloni; koma anauononga konse, ndi amoyo onse anali m'mwemo. Pamenepo Yoswa, ndi Aisraele onse naye, anabwerera kudza ku Debiri, nauthira nkhondo, naulanda, ndi mfumu yake ndi midzi yake yonse; naikantha ndi lupanga lakuthwa, naononga konse amoyo onse anali m'mwemo; sanasiye ndi mmodzi yense; monga anachitira Hebroni momwemo anachitira Debiri ndi mfumu yake, monganso anachitira Libina ndi mfumu yake. Motero Yoswa anakantha dziko lonse, la kumapiri, la kumwera, la kuchidikha, la kuzigwa, ndi mafumu ao onse; sanasiyepo ndi mmodzi yense; koma anaononga psiti zonse zampweya, monga Yehova Mulungu wa Israele adalamulira. Ndipo Yoswa anawakantha kuyambira Kadesi-Baranea mpaka ku Gaza, ndi dziko lonse la Goseni mpaka ku Gibiyoni. Ndipo Yoswa anagwira mafumu awa onse ndi dziko lao nthawi yomweyi; chifukwa Yehova Mulungu wa Israele anathirira Israele nkhondo. Pamenepo Yoswa ndi Aisraele onse naye, anabwerera kuchigono ku Giligala. Ndipo kunali, pamene Yabini mfumu ya ku Hazori anachimva, anatuma kwa Yobabu mfumu ya ku Madoni, ndi kwa mfumu ya ku Simironi, ndi kwa mfumu ya ku Akisafu, ndi kwa mafumu akukhala kumpoto kumapiri, ndi kuchigwa kumwera kwa Kineroti, ndi kuchidikha, ndi ku mitunda ya Dori kumadzulo; kwa Akanani kum'mawa ndi kumadzulo, ndi kwa Aamori ndi Ahiti, ndi Aperizi ndi Ayebusi kumapiri, ndi kwa Ahivi kunsi kwa Heremoni, m'dziko la Mizipa. Ndipo anatuluka, iwo ndi makamu ao onse nao, anthu ambiri, kuchuluka kwao ngati mchenga uli m'mphepete mwa nyanja; ndi akavalo ndi magaleta ambirimbiri. Ndipo mafumu awa onse anasonkhana, nadza namanga pamodzi ku madzi a Meromu, kumthira Israele nkhondo. Koma Yehova anati kwa Yoswa, Usaope chifukwa cha iwowa; pakuti mawa, dzuwa lino ndidzawapereka onse ophedwa pamaso pa Israele; uziwadula mitsindo akavalo ao, ndi kutentha agaleta ao ndi moto. Ndipo Yoswa, ndi anthu onse a nkhondo naye, anawadzera modzidzimutsa ku madzi a Meromu, nawagwera. Ndipo Yehova anawapereka m'dzanja la Israele, ndipo anawakantha, nawapirikitsa mpaka ku Sidoni waukulu, ndi ku Misirefoti-Maimu, ndi ku chigwa cha Mizipa ku m'mawa; nawakantha mpaka sanawasiyire ndi mmodzi yense. Ndipo Yoswa anawachitira monga Yehova adamuuza: nadula akavalo ao mitsindo, natentha magaleta ao ndi moto. Ndipo Yoswa anabwerera m'mbuyo nthawi imeneyi nalanda Hazori nakantha mfumu yake ndi lupanga; pakuti kale Hazori unali waukulu wa maufumu aja onse. Ndipo anakantha amoyo onse anali m'mwemo, ndi lupanga lakuthwa, ndi kuwaononga konse, osasiyapo ndi mmodzi yense wakupuma mpweya; ndipo anatentha Hazori ndi moto. Ndipo Yoswa analanda midzi yonse ya mafumu awa, ndi mafumu ao omwe nawakantha ndi lupanga lakuthwa, nawaononga konse; monga Mose mtumiki wa Yehova adalamulira. Koma midzi yonse yomangidwa pa zitunda zao Israele sanaitenthe, koma wa Hazori wokha; umenewu Yoswa anautentha. Ndi zofunkha zonse za midzi iyi ndi ng'ombe ana a Israele anadzifunkhira; koma anakantha ndi lupanga lakuthwa anthu onse mpaka adawaononga osasiyapo ndi mmodzi yense wopuma mpweya. Monga Yehova adalamulira Mose mtumiki wake, momwemo Mose analamulira Yoswa; momwemonso anachita Yoswa; sanachotsepo mau amodzi pa zonse Yehova adalamulira Mose. Motero Yoswa analanda dziko lonselo, la kumapiri, ndi la kumwera, ndi dziko lonse la Goseni, ndi dziko la kuchidikha, ndi la kuchigwa; ndi la kumapiri la Israele, ndi la ku chidikha chake; kuyambira phiri la Halaki lokwera kunka ku Seiri, mpaka Baala-Gadi m'chigwa cha Lebanoni patsinde pa phiri la Heremoni; nagwira mafumu ao onse, nawakantha, nawapha. Yoswa anathira nkhondo mafumu awa onse nthawi yaikulu. Palibe mudzi wakupangana mtendere ndi ana a Israele, koma Ahivi okhala m'Gibiyoni; anaigwira yonse ndi nkhondo. Pakuti chidadzera kwa Yehova kulimbitsa mitima yao kuti athirane nao Aisraele nkhondo kuti Iye awaononge konse, kuti asawachitire chifundo koma awaononge, monga Yehova adalamulira Mose. Ndipo Yoswa anadza nthawi yomweyo, napasula Aanaki kuwachotsa kumapiri, ku Hebroni, ku Debiri, ku Anabu, ndi ku mapiri onse a Yuda, ndi ku mapiri onse a Israele; Yoswa anawaononga konse, ndi midzi yao yomwe. Panalibe Aanaki otsala m'dziko la ana a Israele; koma m'Gaza ndi m'Gati ndi m'Asidodi anatsalamo ena. Motero Yoswa analanda dziko lonse monga mwa zonse Yehova adazinena kwa Mose; ndipo Yoswa analipereka kwa Israele, likhale laolao, fuko lililonse gawo lake. Ndipo dziko linapumula nkhondo. Ndipo awa ndi mafumu a dzikolo amene ana a Israele anawakantha, nalanda dziko lao tsidya la Yordani kum'mawa, kuyambira chigwa cha Arinoni, mpaka phiri la Heremoni, ndi chidikha chonse cha kum'mawa; Sihoni mfumu ya Aamori wokhala m'Hesiboni, wochita ufumu kuyambira ku Aroere ndiwo m'mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndi pakati pa chigwa ndi pa Giliyadi wogawika pakati, kufikira mtsinje wa Yaboki, ndiwo malire a ana a Amoni; ndi pachidikha mpaka nyanja ya Kineroti kum'mawa, ndi mpaka nyanja ya kuchidikha, ndiyo Nyanja ya Mchere kum'mawa, njira ya Beteyesimoti; ndi kumwera pansi pa matsikiro a Pisiga. Nalandanso malire a Ogi mfumu ya Basani wotsala wa Arefaimu, wokhala ku Asitaroti ndi ku Ederei, nachita ufumu m'phiri la Heremoni, ndi m'Saleka, ndi m'Basani lonse, mpaka malire a Agesuri, ndi a Maakati, ndi Giliyadi wogawika pakati, malire a Sihoni mfumu ya ku Hesiboni. Mose mtumiki wa Yehova ndi ana a Israele anawakantha; ndi Mose mtumiki wa Yehova analipereka kwa Arubeni, ndi Agadi ndi fuko la Manase logawika pakati, likhale cholowa chao. Ndipo awa ndi mafumu a dzikolo amene Yoswa ndi ana a Israele anawakantha tsidya lija la Yordani kumadzulo, kuyambira Baala-Gadi m'chigwa cha Lebanoni mpaka phiri la Halaki lokwera kunka ku Seiri; ndipo Yoswa analipereka kwa mafuko a Israele, likhale laolao, monga mwa magawo ao; kumapiri ndi kuchigwa, ndi kuchidikha, ndi kumatsikiro, ndi kuchipululu, ndi kumwera: Ahiti, Aamori, ndi Akanani, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi: mfumu ya ku Yeriko, imodzi; mfumu ya ku Ai, ndiwo m'mbali mwa Betele, imodzi; mfumu ya ku Yerusalemu, imodzi; mfumu ya ku Hebroni, imodzi; mfumu ya ku Yaramuti, imodzi; mfumu ya ku Lakisi, imodzi; mfumu ya ku Egiloni, imodzi; mfumu ya ku Gezere, imodzi; mfumu ya ku Debiri, imodzi; mfumu ya ku Gederi, imodzi; mfumu ya ku Horoma, imodzi; mfumu ya ku Aradi, imodzi; mfumu ya ku Libina, imodzi; mfumu ya ku Adulamu, imodzi; mfumu ya ku Makeda, imodzi; mfumu ya ku Betele, imodzi; mfumu ya ku Tapuwa, imodzi; mfumu ya ku Hefere, imodzi; mfumu ya ku Afeki, imodzi; mfumu ya ku Lasaroni, imodzi; mfumu ya ku Madoni, imodzi; mfumu ya ku Hazori, imodzi; mfumu ya ku Simironi-Meroni, imodzi; mfumu ya ku Akisafu, imodzi; mfumu ya ku Taanaki, imodzi; mfumu ya ku Megido, imodzi; mfumu ya ku Kedesi, imodzi; mfumu ya ku Yokoneamu ku Karimele, imodzi; mfumu ya ku Dori, mpaka ponyamuka pa Dori, imodzi; mfumu ya ku Goimu m'Galileya, imodzi; mfumu ya ku Tiriza, imodzi. Mafumu awa onse ndiwo makumi atatu ndi imodzi. Ndipo Yoswa anakalamba, wa zaka zambiri; ndipo Yehova ananena naye, Wakalamba, wa zaka zambiri, ndipo latsala dziko lalikulukulu, alilandire cholowa chao. Dziko lotsala ndilo: malire onse a Afilisti, ndi Agesuri onse, kuyambira Sihori wokhala chakuno cha Ejipito mpaka malire a Ekeroni kumpoto, loyesedwa la Akanani; akalonga asanu a Afilisti, a ku Gaza, ndi a ku Asidodi, a ku Asikeloni, a ku Gati, ndi a ku Ekiro, ndi Avimu; kumwera dziko lonse la Akanani, ndi Meara ndiwo wa Asidoni, mpaka ku Afeki, mpaka ku malire a Aamori; ndi dziko la Agebala, ndi Lebanoni, lonse kum'mawa, kuyambira Baala-Gadi pa tsinde la phiri la Heremoni, mpaka polowera pake pa Hamati; nzika zonse za kumapiri kuyambira Lebanoni, mpaka Misirefoti-Maimu, Asidoni onse; ndidzawainga pamaso pa ana a Israele, koma limeneli uwagawire Aisraele, likhale cholowa chao, monga ndinakulamulira. Ndipo tsopano uwagawire mafuko asanu ndi anai, ndi fuko la Manase logawika pakati, dziko ili likhale cholowa chao. Pamodzi ndi iye Arubeni ndi Agadi analandira cholowa chao, chimene Mose adawapatsa tsidya ilo la Yordani kum'mawa, monga Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa; kuyambira pa Aroere, wokhala m'mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndi mudzi uli pakati pa chigwa, ndi chidikha chonse cha Medeba mpaka ku Diboni; ndi midzi yonse ya Sihoni mfumu ya Aamori, wakuchita ufumu m'Hesiboni, mpaka malire a ana a Amoni; ndi Giliyadi, ndi malire a Agesuri, ndi Amaakati, ndi phiri lonse la Heremoni, ndi Basani lonse mpaka ku Saleka; ufumu wonse wa Ogi m'Basani, wa kuchita ufumu m'Asitaroti, ndi m'Ederei (yemweyo anatsala pa otsala a Arefaimu); pakuti Mose anakantha awa, nawainga. Koma ana a Israele sanainge Agesuri kapena Amaakati; koma Gesuri, ndi Maakati amakhala pakati pa Israele, mpaka lero lino. Koma fuko la Levi sanalipatse cholowa; nsembe za Yehova Mulungu wa Israele, zochitika ndi moto, ndizo cholowa chake, monga Iye adanena naye. Ndipo Mose anapatsira fuko la ana a Rubeni monga mwa mabanja ao. Malire ao anayambira ku Aroere wokhala m'mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndi mudzi uli pakati pa chigwa ndi chidikha chonse cha ku Medeba; Hesiboni ndi midzi yake yonse yokhala pachidikha; Diboni, ndi Bamoti-Baala ndi Bete-Baala-Meoni; ndi Yahazi ndi Kedemoti, ndi Mefaati; ndi Kiriyataimu, ndi Sibima, ndi Zeretisahara, m'phiri la kuchigwa; ndi Betepeori, ndi matsikiro a Pisiga, ndi Beteyesimoti; ndi midzi yonse ya kuchidikha, ndi ufumu wonse wa Sihoni mfumu ya Aamori, wochita ufumu m'Hesiboni, amene Mose anamkantha pamodzi ndi akalonga a Midiyani, Evi, ndi Rekemu, ndi Zuri, ndi Huri ndi Reba, akalonga a Sihoni, nzika za m'dziko. Ana a Israele anaphanso ndi lupanga Balamu mwana wa Beori, mlauli uja, pamodzi ndi ena adawaphawo. Ndipo malire a ana a Rubeni ndiwo Yordani ndi malire ake. Ndicho cholandira cha ana a Rubeni monga mwa mabanja ao, midzi yake ndi milaga yake. Ndipo Mose anapatsira fuko la Gadi, ana a Gadi, monga mwa mabanja ao. Ndipo malire ao ndiwo Yazere, ndi midzi yonse ya Giliyadi, ndi dziko la ana a Amoni logawika pakati, mpaka ku Aroere, wokhala chakuno cha Raba; ndi kuyambira Hesiboni mpaka Ramati-Mizipe, ndi Betonimu; ndi kuyambira Mahanaimu mpaka malire a Debiri; ndipo m'chigwa Beteharamu, ndi Betenimura, ndi Sukoti, ndi Zafoni, chotsala cha ufumu wa Sihoni mfumu ya Hesiboni, Yordani ndi malire ake, mpaka malekezero a nyanja ya Kinereti, tsidya lija la Yordani kum'mawa. Ichi ndi cholowa cha ana a Gadi, monga mwa mabanja ao, midzi yake ndi milaga yake. Mose anaperekanso cholowa kwa fuko la Manase logawika pakati, ndicho cha fuko la Manase logawika pakati monga mwa mabanja ao. Ndipo malire ao anayambira ku Mahanaimu, Basani lonse, ufumu wonse wa Ogi mfumu ya ku Basani, ndi midzi yonse ya Yairi, yokhala m'Basani, midzi makumi asanu ndi limodzi; ndi Giliyadi logawika pakati, ndi Asitaroti ndi Ederei, midzi ya ufumu wa Ogi m'Basani, inali ya ana a Makiri mwana wa Manase, ndiwo ana a Makiri ogawika pakati, monga mwa mabanja ao. Izi ndi zolowazi Mose anazigawira m'zidikha za Mowabu, tsidya ilo la Yordani ku Yeriko, kum'mawa. Koma fuko la Levi, Mose analibe kulipatsa cholowa: Yehova Mulungu wa Israele, ndiye cholowa chao, monga ananena nao. Ndipo awa ndi maiko ana a Israele anawalanda m'dziko la Kanani, amene Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a nyumba za atate a mafuko a ana a Israele, anawagawira. Kulandira kwao kunachitika ndi kulota maere, monga Yehova adalamulira mwa dzanja la Mose, kunena za mafuko asanu ndi anai ndi fuko logawika pakati. Pakuti Mose adapatsa mafuko awiri, ndi fuko logawika pakati, cholowa tsidya ilo la Yordani; koma sanapatse Alevi cholowa pakati pao. Pakuti ana a Yosefe ndiwo mafuko awiri, Manase ndi Efuremu; ndipo sanawagawire Alevi kanthu m'dziko, koma midzi yokhalamo ndi dziko lozungulirako likhale la zoweta zao ndi chuma chao. Monga Yehova analamulira Mose, momwemo ana a Israele anachita, nagawana dziko. Pamenepo ana a Yuda anadza kwa Yoswa ku Giligala; ndi Kalebe mwana wa Yefune Mkenizi ananena naye, Mudziwa chimene Yehova adanena kwa Mose munthu wa Mulungu za ine ndi za inu m'Kadesi-Baranea. Ndinali ine wa zaka makumi anai muja Mose mtumiki wa Yehova anandituma kuchokera ku Kadesi-Baranea, kukazonda dziko; ndipo ndinambwezera mau, monga momwe anakhala mumtima mwanga. Koma abale anga amene anakwera nane anasungunutsa mitima ya anthu; koma ine ndinamtsata Yehova Mulungu wanga ndi mtima wanga wonse. Ndipo Mose analumbira tsiku lomwelo ndi kuti, Zedi, dzikoli phazi lako lapondapo lidzakhala cholowa chako, ndi cha ana ako kosalekeza, chifukwa unatsata Yehova Mulungu wanga ndi mtima wonse. Ndipo tsopano, taonani, Yehova anandisunga ndi moyo, monga ananena, zaka izi makumi anai ndi zisanu kuyambira nthawi ija Yehova ananena kwa Mose mau awa, poyenda Israele m'chipululu; ndipo tsopano taonani, ndine wa zaka makumi asanu ndi atatu, kudza zisanu lero lino. Koma lero lino ndili wamphamvu monga tsiku lija anandituma Mose; monga mphamvu yanga pamene paja, momwemo mphamvu yanga tsopano, kugwira nkhondo, ndi kutuluka ndi kulowa. Ndipo tsopano, ndipatseni phiri ili limene Yehova ananenera tsiku lija; pakuti udamva tsiku lijalo kuti Aanaki anali komweko, ndi midzi yaikulu ndi yamalinga; kapena Yehova adzakhala ndi ine, kuti ndiwaingitse monga ananena Yehova. Pamenepo Yoswa anamdalitsa, napatsa Kalebe mwana wa Yefune Hebroni likhale cholowa chake. Chifukwa chake Hebroni likhala cholowa chake cha Kalebe mwana wa Yefune Mkenizi mpaka lero lino; popeza anatsata Yehova Mulungu wa Israele ndi mtima wonse. Koma kale dzina la Hebroni linali mudzi wa Araba, ndiye munthu wamkulu pakati pa Aanaki. Ndipo dziko linapumula nkhondo. Ndipo gawo la fuko la ana a Yuda monga mwa mabanja ao linafikira malire a Edomu, ku chipululu cha Zini kumwera, ku malekezero a kumwera. Ndi malire ao a kumwera, anayambira ku malekezero a Nyanja ya Mchere, ku nyondo yoloza kumwera; natuluka kumwera kwa chikweza cha Akarabimu, napitirira ku Zini, nakwera kumwera kwa Kadesi-Baranea, napitirira ku Hezironi, nakwera ku Adara, nazungulira ku Karika; napitirira ku Azimoni, natuluka ku mtsinje wa Ejipito; ndi malekezero a malirewa anali ku Nyanja Yaikulu; awa ndi malire anu a kumwera. Ndi malire a kum'mawa ndiwo Nyanja ya Mchere, mpaka mathiriro ake a Yordani. Ndi malire a kumpoto anayambira nyondo ya nyanja ku mathiriro a Yordani; nakwera malire kunka ku Betehogila, napitirira kumpoto kwa Betaraba; nakwera malire kunka ku mwala wa Bohani mwana wa Rubeni; nakwera malire kunka ku Debiri, kuchokera ku chigwa cha Akori, ndi kumpoto kupenyera Giligala ndiko kundunji kwa chikweza cha Adumimu, ndiko kumwera kwa mtsinje; napitirira malire kunka ku madzi a Enisemesi, ndi matulukiro ake anali ku Enirogele; nakwera malire kunka ku chigwa cha mwana wa Hinomu, kumbali kwa Ayebusi, kumwera, ndiko Yerusalemu; nakwera malire kunka kumwamba kwa phiri lokhala patsogolo pa chigwa cha Hinomu kumadzulo, ndilo ku mathero ake a chigwa cha Refaimu kumpoto. Ndipo analemba malire kuyambira pamwamba pa phiri mpaka chitsime cha madzi cha Nefitowa, natulukira malire kumidzi ya phiri la Efuroni; ndipo analemba malire kunka ku Baala, ndiwo Kiriyati-Yearimu. Ndipo malire anazungulira kuyambira ku Baala kunka kumadzulo, kuphiri la Seiri, napitirira kumbali kwa phiri la Yearimu kumpoto, ndilo Kesaloni, natsikira ku Betesemesi, napitirira ku Timna; natuluka malire kunka ku mbali ya Ekeroni kumpoto; ndipo analemba malire kunka ku Sikeroni, napitirira kuphiri la Baala, natuluka ku Yabinele; ndipo matulukiro a malire anali kunyanja. Ndi malire a kumadzulo anali ku Nyanja Yaikulu ndiwo malire ake. Awa ndi malire a ana a Yuda pozungulira monga mwa mabanja ao. Koma Yoswa anampatsa Kalebe mwana wa Yefune gawo mwa ana a Yuda, monga Yehova adamlamulira, ndiwo mudzi wa Araba, ndiye atate wa Anaki, ndiwo Hebroni. Ndipo Kalebe anaingitsako ana amuna atatu a Anaki, ndiwo Sesai, ndi Ahimani, ndi Talimai, ana a Anaki. Nakwera komweko kunka kwa nzika za Debiri; koma kale dzina la Debiri ndilo Kiriyati-Sefere. Ndipo Kalebe anati, Iye amene akantha Kiriyati-Sefere, naulanda, yemweyo ndidzampatsa Akisa mwana wanga akhale mkazi wake. Ndipo Otiniyele mwana wa Kenazi, mbale wake wa Kalebe, anaulanda; ndipo anampatsa Akisa mwana wake akhale mkazi wake. Ndipo kunali, m'mene anamdzera, anamkangamiza mwamuna wake kuti apemphe atate wake ampatse munda; ndipo anatsika pa bulu; pamenepo Kalebe ananena naye, Ufunanji? Nati iye, Mundipatse dalitso; popeza mwandipatsa dziko la kumwera, ndipatseninso zitsime za madzi. Pamenepo anampatsa zitsime za kumtunda, ndi zitsime za kunsi. Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Yuda monga mwa mabanja ao. Ndipo midzi ya ku malekezero a fuko la ana a Yuda ku malire a Edomu, kumwera ndiwo, Kabizeeli ndi Edere, ndi Yaguru; ndi Kina ndi Dimona, ndi Adada; ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Itinani; Zifi ndi Telemu ndi Bealoti; ndi Hazori-Hadata, ndi Keriyoti-Hezironi, ndiwo Hazori; Amama ndi Sema ndi Molada; ndi Hazara-Gada, ndi Hesimoni, ndi Betepeleti; ndi Hazara-Suwala, ndi Beereseba, ndi Biziyotiya; Baala, ndi Iyimu, ndi Ezemu; ndi Elitoladi, ndi Kesili ndi Horoma; ndi Zikilagi, ndi Madimana ndi Sanisana; ndi Lebaoti, ndi Silihimu, ndi Aini ndi Rimoni; midzi yonse ndiyo makumi awiri kudza isanu ndi inai; pamodzi ndi milaga yao. Ku chigwa, Esitaoli, ndi Zora ndi Asina; ndi Zanowa, ndi Enganimu, Tapuwa, ndi Enamu; Yaramuti, ndi Adulamu, Soko, ndi Azeka; ndi Saaraimu, ndi Aditaimu, ndi Gedera, ndi Gederotaimu; midzi khumi ndi inai pamodzi ndi milaga yao. Zenani, ndi Hadasa, ndi Megidali-Gadi; ndi Dileani, ndi Mizipa, ndi Yokotele; Lakisi ndi Bozikati ndi Egiloni; ndi Kaboni, ndi Lahamasi, ndi Kitilisi; ndi Gederoti, Betedagoni, ndi Naama, ndi Makeda; midzi khumi ndi isanu ndi umodzi pamodzi ndi milaga yao. Libina ndi Eteri ndi Asani; ndi Ifuta ndi Asina ndi Nezibu; ndi Keila ndi Akizibu, ndi Maresa; midzi isanu ndi inai pamodzi ndi milaga yao. Ekeroni pamodzi ndi midzi yake ndi milaga yao; kuyambira ku Ekeroni mpaka kunyanja, yonse ya ku mbali ya Asidodi, pamodzi ndi milaga yao. Asidodi, midzi yake ndi milaga yake; Gaza, midzi yake ndi milaga yake; mpaka mtsinje wa Ejipito, ndi Nyanja Yaikulu ndi malire ake. Ndi kumapiri Samiri, ndi Yatiri, ndi Soko; ndi Dana, ndi Kiriyati-Sana, ndiwo Debiri; ndi Anabu, ndi Esitemowa, ndi Animu; ndi Goseni, ndi Holoni, ndi Gilo; midzi khumi ndi umodzi pamodzi ndi milaga yao. Arabu, ndi Duma, ndi Esani; ndi Yanimu, ndi Betetapuwa, ndi Afeka; ndi Humata, ndi Kiriyati-Ariba, ndiwo Hebroni, ndi Ziyori; midzi isanu ndi inai pamodzi ndi milaga yao. Maoni, Karimele, ndi Zifi, ndi Yuta; ndi Yezireele, ndi Yokodeamu, ndi Zanowa; Kaini, Gibea ndi Timna; midzi khumi pamodzi ndi milaga yao. Halahulu, Betezuri, ndi Gedori, ndi Maarati, ndi Betanoti, ndi Elitekoni; midzi isanu ndi umodzi pamodzi ndi milaga yao. Kiriyati-Baala, ndiwo Kiriyati-Yearimu ndi Raba; midzi iwiri pamodzi ndi milaga yao. M'chipululu, Betaraba, Midini, ndi Sekaka; ndi Nibisani, ndi Mudzi wa Mchere, ndi Engedi; midzi isanu ndi umodzi pamodzi ndi milaga yao. Koma ana a Yuda sanakhoze kuingitsa Ayebusi, nzika za Yerusalemu: m'mwemo Ayebusi anakhala pamodzi ndi ana a Yuda, ku Yerusalemu, mpaka lero lino. Ndipo gawo la ana a Yosefe linatuluka kuchokera ku Yordani ku Yeriko, ku madzi a Yeriko kum'mawa, kuchipululu, nakwera kuchokera ku Yeriko kunka kumapiri ku Betele; natuluka ku Betele kunka ku Luzi, napitirira kunka ku malire a Aariki, ku Ataroti; natsikira kumadzulo kunka ku malire a Ayafileti, ku malire a Betehoroni wa kunsi, ndi ku Gezere; ndi matulukiro ake anali kunyanja. Motero ana a Yosefe, Manase ndi Efuremu analandira cholowa chao, Ndipo malire a ana a Efuremu, monga mwa mabanja ao, ndiwo: malire a cholowa chao kum'mawa ndiwo Ataroti-Adara, mpaka Betehoroni wa kumtunda; natuluka malire kumadzulo ku Mikametati kumpoto; nazungulira malire kum'mawa kunka ku Taanatisilo, naupitirira kum'mawa kwake kwa Yanowa: natsika kuchokera ku Yanowa, kunka ku Ataroti, ndi ku Naara, nafika ku Yeriko, natuluka ku Yordani. Kuyambira ku Tapuwa malire anamuka kumadzulo ku mtsinje wa Kana; ndi matulukiro ake anali kunyanja. Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Efuremu monga mwa mabanja ao; pamodzi ndi midzi adaipatulira ana a Efuremu pakati pa cholowa cha ana a Manase, midzi yonse pamodzi ndi milaga yao. Ndipo sanaingitse Akanani akukhala m'Gezere; koma Akanani anakhala pakati pa Efuremu, kufikira lero lino, nawaumiriza kugwira ntchito yathangata. Gawo la fuko la Manase ndi ili: pakuti anali woyamba wa Yosefe. Makiri mwana woyamba wa Manase, atate wa Giliyadi, popeza ndiye munthu wa nkhondo, anakhala nayo Giliyadi ndi Basani. Ndipo maere anagwera ana ena otsala a Manase monga mwa mabanja ao; ana a Abiyezere ndi ana a Heleki, ndi ana a Asiriele, ndi ana a Sekemu ndi ana a Hefere, ndi ana a Semida; awa ndi ana amuna a Manase mwana wa Yosefe, monga mwa mabanja ao. Koma Zelofehadi, mwana wa Hefere, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase, analibe ana amuna koma ana akazi ndiwo; ndipo maina a ana ake akazi ndiwo: Mala, ndi Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza. Ndipo anayandikira pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa Yoswa mwana wa Nuni, ndi pamaso pa akalonga, ndi kuti, Yehova analamulira Mose atipatse cholowa pakati pa abale athu; chifukwa chake anawapatsa monga mwa lamulo la Yehova, cholowa pakati pa abale a atate wao. Ndipo anamgwera Manase magawo khumi, osawerenga dziko la Giliyadi ndi Basani lokhala tsidya lija la Yordani: popeza ana akazi a Manase adalandira cholowa pakati pa ana ake amuna; ndi dziko la Giliyadi linakhala la ana a Manase otsala. Ndipo malire a Manase anayambira ku Asere, kunka ku Mikametati, wokhala chakuno cha Sekemu; namuka malire ku dzanja lamanja kwa nzika za Enitapuwa. Dziko la Tapuwa linali la Manase; koma Tapuwa mpaka malire a Manase linakhala la ana a Efuremu. Natsikira malire ku mtsinje wa Kana, kumwera kwa mtsinje; midzi iyi inakhala ya Efuremu pakati pa midzi ya Manase; ndi malire a Manase anali kumpoto kwa mtsinje; ndi matulukiro ake anali kunyanja; kumwera nkwa Efuremu ndi kumpoto nkwa Manase, ndi malire ake ndi nyanja; ndi kumpoto anakomana ndi Asere, ndi kum'mawa anakomana ndi Isakara. Ndipo m'Isakara ndi m'Asere Manase anali nao Beteseani ndi midzi yake, ndi Ibleamu ndi midzi yake, ndi nzika za Dori ndi midzi yake, ndi nzika za Endori ndi midzi yake, ndi nzika za Taanaki ndi midzi yake, ndi nzika za Megido ndi midzi yake; dziko la mapiri atatu. Koma ana a Manase sanathe kuingitsa a m'midzi aja, popeza Akanani anafuna kukhala m'dziko lija. Ndipo kunali pamene ana a Israele atakula mphamvu anasonkhetsa Akanani osawaingitsa onse. Pamenepo ana a Yosefe ananena ndi Yoswa, ndi kuti, Watipatsiranji cholowa chathu chamaere chimodzi ndi gawo limodzi, popeza ife ndife anthu aunyinji, pakuti Yehova anatidalitsa ndi pano pomwe? Ndipo Yoswa ananena nao, Ngati muli anthu aunyinji, kwerani kuli mitengoko, ndi kudziswera minda m'dziko la Aperizi ndi la Arefaimu; akakucheperani malo kuphiri la Efuremu. Ndipo ana a Yosefe anati, Ku phiriko sikudzatifikira; ndipo Akanani onse akukhala m'dziko la chigwa ali nao magaleta achitsulo, iwo akukhala m'Beteseani, ndi midzi yake ndi iwo omwe akukhala m'chigwa cha Yezireele. Ndipo Yoswa ananena kwa iwo a m'nyumba ya Yosefe, kwa Efuremu ndi Manase, ndi kuti, Inu ndinu anthu aunyinji, muli nayo mphamvu yaikulu; simudzakhala nalo gawo limodzi lokha; koma kuphiriko kudzakhala kwanu pakuti pangakhale mpa mitengo, mudzisweretu minda, ndi matulukiro ake adzakhala anu; pakuti mudzaingitsa Akanani angakhale ali nao magaleta achitsulo, angakhale ali amphamvu. Ndipo msonkhano wonse wa ana a Israele unasonkhana ku Silo, nuutsa komweko chihema chokomanako; ndipo dziko linawagonjera. Ndipo anatsala mwa ana a Israele mafuko asanu ndi awiri osawagawira cholowa chao. Ndipo Yoswa anati kwa ana a Israele, Muchedwa mpaka liti kulowa ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu anakupatsani? Mudzifunire amuna, fuko lililonse amuna atatu; kuti ndiwatume, anyamuke, nayendeyende iwo pakati pa dziko, nalilembe monga mwa cholowa chao; nabwerenso kwa ine. Ndipo adzaligawa magawo asanu ndi awiri; Yuda adzakhala m'malire ake kumwera, ndi a m'nyumba ya Yosefe adzakhala m'malire mwao kumpoto. Ndipo muzilemba dziko likhale magawo asanu ndi awiri, ndi kubwera nao kuno kwa ine malembo ake; ndipo ndidzakuloterani maere pano pamaso pa Yehova Mulungu wathu. Pakuti Alevi alibe gawo pakati pa inu; pakuti unsembe wa Yehova ndiwo cholowa chao. Koma Gadi, ndi Rubeni, ndi fuko la Manase logawika pakati adalandira cholowa chao tsidya lija la Yordani kum'mawa, chimene Mose mtumiki wa Yehova adawapatsa. Ndipo amunawo ananyamuka, namuka; ndipo Yoswa analamulira opita kulemba dzikowo, ndi kuti, Mukani, muyendeyende pakati pa dziko, ndi kulilemba, nimubwerenso kwa ine, ndipo ndidzakuloterani maere pano pamaso pa Yehova pa Silo. Namuka amunawo, napitapita pakati pa dziko, nalilemba m'buku, nayesa midzi yake, magawo asanu, nabwera kwa Yoswa ku chigono ku Silo. Ndipo Yoswa anawalotera maere ku Silo pamaso pa Yehova; ndi apo Yoswa anawagawira ana a Israele dziko, monga mwa magawo ao. Ndipo maere a fuko la ana a Benjamini anakwera monga mwa mabanja ao; ndi malire a gawo lao anatuluka pakati pa ana a Yuda ndi ana a Yosefe. Ndipo malire ao a kumpoto anachokera ku Yordani; ndi malire anakwera ku mbali ya Yeriko kumpoto, nakwera pakati pa mapiri kumadzulo; ndi matulukiro ake anali ku chipululu cha Betaveni. Ndipo malire anapitirirapo kunka ku Luzi, ku mbali ya Luzi, momwemo ndi Betele, kumwera; ndi malire anatsikira kunka ku Ataroti-Adara, kuphiri lokhala kumwera kwa Betehoroni wa kunsi. Ndipo malire analembedwa nazungulira ku mbali ya kumadzulo kunka kumwera, kuchokera kuphiri pokhala patsogolo pa Betehoroni, kumwera kwake; ndi matulukiro ake anali ku Kiriyati-Baala, womwewo ndi Kiriyati-Yearimu, mudzi wa ana a Yuda; ndiyo mbali ya kumadzulo. Ndipo mbali ya kumwera inayambira polekezera Kiriyati-Yearimu; natuluka malire kunka kumadzulo, natuluka kunka ku chitsime cha madzi a Nefitowa; natsikira malire kunka polekezera phiri lokhala patsogolo pa chigwa cha mwana wa Hinomu, ndicho cha m'chigwa cha Refaimu kumpoto; natsikira ku chigwa cha Hinomu, ku mbali ya Ayebusi kumwera, natsikira ku Enirogele; nalembedwa kunka kumpoto, natuluka ku Enisemesi, natuluka ku Geliloti, ndiwo pandunji pokwerera pa Adumimu; natsikira ku mwala wa Bohani mwana wa Rubeni; napitirira ku mbali ya pandunji pa Betaraba kumpoto, natsirika kunka ku Araba; napitirira malire kunka ku mbali ya Betehogila kumpoto; ndi matulukiro ake a malire anali ku nyondo ya kumpoto ya Nyanja ya Mchere; pa kulekezera kwa kumwera kwa Yordani; ndiwo malire a kumwera. Ndipo malire ake mbali ya kum'mawa ndiwo Yordani, ndicho cholowa cha ana a Benjamini, kunena za malire ake pozungulira pake, monga mwa mabanja ao. Koma midzi ya fuko la ana a Benjamini monga mwa mabanja ao ndiyo Yeriko, ndi Betehogila, ndi Emekezizi; ndi Betaraba, ndi Zemaraimu, ndi Betele; ndi Avimu ndi Para, ndi Ofura; ndi Kefaramoni, ndi Ofini, ndi Geba; midzi khumi ndi iwiri pamodzi ndi milaga yao; Gibiyoni ndi Rama, ndi Beeroti; ndi Mizipa, ndi Kefira, ndi Moza; ndi Rekemu, ndi Iripele ndi Tarala; ndi Zela, Haelefe, ndi Yebusi, womwewo ndi Yerusalemu, Gibea ndi Kiriyati-Yearimu; midzi khumi ndi inai pamodzi ndi milaga yake. Ndicho cholowa cha ana a Benjamini monga mwa mabanja ao. Ndipo maere achiwiri anamtulukira Simeoni, fuko la ana a Simeoni monga mwa mabanja ao; ndi cholowa chao chinali pakati pa cholowa cha ana a Yuda. Ndipo anali nacho cholowa chao Beereseba, kapena Sheba, ndi Molada; ndi Hazara-Suwala, ndi Bala, ndi Ezemu; ndi Elitoladi, ndi Betuli, ndi Horoma; ndi Zikilagi, ndi Betemara-Kaboti, ndi Hazara-Susa: ndi Betelebaoti, ndi Saruheni; midzi khumi ndi itatu ndi milaga yao; Aini, Rimoni ndi Eteri ndi Asani; midzi inai ndi milaga yao; ndi milaga yonse yozungulira midzi iyi mpaka Baalati-Bere ndiwo Rama kumwera. Ndicho cholowa cha fuko la ana a Simeoni, monga mwa mabanja ao. M'gawo la ana a Yuda muli cholowa cha ana a Simeoni; popeza gawo la ana a Yuda linawachulukira; chifukwa chake ana a Simeoni anali nacho cholowa pakati pa cholowa chao. Ndipo maere achitatu anakwerera ana a Zebuloni monga mwa mabanja ao; ndi malire a cholowa chao anafikira ku Saridi; nakwera malire ao kunka kumadzulo ndi ku Mareyala nafikira ku Dabeseti, nafikira ku mtsinje wa patsogolo pa Yokoneamu; ndi kuchokera ku Saridi anazungulira kunka kum'mawa kumatulukira dzuwa, mpaka malire a Kisiloti-Tabori; natuluka kunka ku Daberati, nakwera ku Yafiya; ndi pochoka pamenepo anapitirira kunka kum'mawa ku Gatihefere, ku Etikazini; natuluka ku Rimoni umene ulembedwa mpaka ku Neya, nauzungulira malire kumpoto, kunka ku Hanatoni; ndi matulukiro ake anali ku chigwa cha Ifutahele; ndi Katati, ndi Nahalala ndi Simironi, ndi Idala ndi Betelehemu: midzi khumi ndi iwiri ndi milaga yao. Ichi ndi cholowa cha ana a Zebuloni monga mwa mabanja ao, midzi iyi ndi milaga yao. Maere achinai anamtulukira Isakara, kunena za ana a Isakara monga mwa mabanja ao. Ndi malire ao anali ku Yezireele, ndi Kesuloti, ndi Sunemu; ndi Hafaraimu, ndi Siyoni, ndi Anaharati; ndi Rabiti ndi Kisiyoni, ndi Ebezi; ndi Remeti ndi Enganimu ndi Enihada, ndi Betepazezi; ndi malire anafikira ku Tabori, ndi Sahazuma, ndi Betesemesi; ndi matulukiro a malire ao anali ku Yordani; midzi khumi ndi isanu ndi umodzi ndi milaga yao. Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Isakara, monga mwa mabanja ao, midzi ndi milaga yao. Ndipo maere achisanu analitulukira fuko la ana a Asere monga mwa mabanja ao. Ndi malire ao ndiwo Helekati, ndi Hali, ndi Beteni ndi Akisafu; ndi Alamumeleki, ndi Amada, ndi Misala; nafikira ku Karimele kumadzulo ndi ku Sihori-Libinati; nazungulira kotulukira dzuwa ku Betedagoni, nafikira ku Zebuloni ndi ku chigwa cha Ifutahele, kumpoto ku Betemeke, ndi Neiyeli; natulukira ku Kabulu kulamanzere, ndi Ebroni, ndi Rehobu, ndi Hamoni, ndi Kana, mpaka ku Sidoni wamkulu; nazungulira malire kunka ku Rama, ndi kumudzi wa linga la Tiro; nazungulira malire kunka ku Hosa; ndi matulukiro ake anali kunyanja, kuchokera ku Mahalabu mpaka ku Akizibu; Uma womwe ndi Afeki, ndi Rehobu; midzi makumi awiri mphambu iwiri ndi milaga yao. Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Asere monga mwa mabanja ao, midzi iyi ndi milaga yao. Maere achisanu ndi chimodzi anatulukira ana a Nafutali, ana a Nafutali monga mwa mabanja ao. Ndipo malire ao anayambira ku Helefe ku thundu wa ku Zaananimu, ndi Adami-Nekebu, ndi Yabinele, mpaka ku Lakumu; ndi matulukiro ake anali ku Yordani; nazungulira malire kunka kumadzulo ku Azinoti-Tabori, natulukira komweko kunka ku Hukoku; nafikira ku Zebuloni kumwera, nafikira ku Asere kumadzulo, ndi ku Yuda pa Yordani kum'mawa. Ndipo midzi yamalinga ndiyo Zidimu, Zeri, ndi Hamati, Rakati, ndi Kinereti; ndi Adama, ndi Rama, ndi Hazori; ndi Kedesi, ndi Ederei, ndi Enihazori; ndi Yironi, ndi Migidalele, Horemu, ndi Betanati, ndi Betesemesi; midzi khumi ndi isanu ndi inai, ndi milaga yao. Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Nafutali, monga mwa mabanja ao, midzi ndi milaga yao. Maere achisanu ndi chiwiri anatulukira fuko la ana a Dani, monga mwa mabanja ao. Ndipo malire a cholowa chao anali Zora, ndi Esitaoli, ndi Irisemesi; Saalabini, ndi Ayaloni ndi Itila; ndi Eloni ndi Timna ndi Ekeroni; ndi Eliteke, ndi Gibetoni, ndi Baalati; ndi Yehudi, ndi Beneberaki, ndi Gatirimoni; ndi Meyarikoni, ndi Rakoni, ndi malire pandunji pa Yopa. Koma malire a ana a Dani anatuluka kupitirira iwowa; pakuti ana a Dani anakwera nathira nkhondo ku Lesemu, naulanda naukantha ndi lupanga lakuthwa, naulandira, nakhala m'mwemo, nautcha Lesemu, Dani; ndilo dzina la Dani atate wao. Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Dani, monga mwa mabanja ao, midzi iyi ndi milaga yao. Ndipo atatha kuligawa dziko likhale cholowa chao monga mwa malire ake, ana a Israele anapatsa Yoswa mwana wa Nuni cholowa pakati pao; monga mwa lamulo la Yehova anampatsa mudzi umene anawapempha, ndiwo Timnati-Sera, ku mapiri a Efuremu; ndipo anamanga mudziwo nakhala m'mwemo. Izi ndizo zolowa anazigawa Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a nyumba za atate a mafuko a ana a Israele, zikhale zaozao, ndi kulota maere ku Silo pamaso pa Yehova ku khomo la chihema chokomanako. Momwemo anatha kuligawa dziko. Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, Nena ndi ana a Israele ndi kuti, Mudziikire midzi yopulumukirako, monga ndinanena kwa inu mwa dzanja la Mose. Kuti athawireko wakupha munthu osamupha dala, osadziwa; ndipo idzakhalire inu yopulumukirako, kumpulumuka wolipsa mwazi. Munthu akathawira umodzi wa midzi iyi, aziima polowera pa chipata cha mudziwo, nafotokozere mlandu wake m'makutu a akulu a mudziwo; pamenepo azimlandira kumudzi kwao, ndi kumpatsa malo, kuti akhale pakati pao. Ndipo akamlondola wolipsa mwazi, asampereke m'dzanja lake wakupha mnzakeyo; pakuti anakantha mnansi wake mosadziwa, osamuda kale. Ndipo azikhala m'mudzimo mpaka adzaima pamaso pa msonkhano anene mlandu wake, mpaka atafa mkulu wa ansembe wa m'masiku omwewo; pamenepo wakupha mnzake azibwerera ndi kufika kumudzi kwake, ndi nyumba yake, kumudzi kumene adathawako. Ndipo anapatula Kedesi m'Galileya ku mapiri a Nafutali, ndi Sekemu ku mapiri a Efuremu, ndi mudzi wa Ariba ndiwo Hebroni ku mapiri a Yuda. Ndipo tsidya lija la Yordani kum'mawa kwa Yeriko, anaika Bezeri m'chipululu, kuchidikha, wa fuko la Rubeni, ndi Ramoti m'Giliyadi wa fuko la Gadi, ndi Golani m'Basani wa fuko la Manase. Iyi ndi midzi yoikidwira ana onse a Israele, ndi mlendo wakukhala pakati pao kuti athawireko aliyense wakupha munthu, ndi kuti asafe ndi dzanja la wolipsa mwazi, asanaime pamaso pa msonkhano. Pamenepo akulu a nyumba za atate a Alevi anayandikira kwa Eleazara wansembe, ndi kwa Yoswa mwana wa Nuni, ndi kwa akulu a nyumba za atate a mafuko a ana a Israele; nanena nao ku Silo m'dziko la Kanani, ndi kuti Yehova analamulira mwa dzanja la Mose kuti atipatse midzi yokhalamo ife, ndi mabusa a zoweta zathu. Ndipo ana a Israele anapatsa Alevi, kutapa pa cholowa chao, monga mwa lamulo la Yehova, midzi iyi ndi mabusa ao. Ndipo maere anatulukira mabanja a Akohati; ndipo molota maere ana a Aroni wansembe, ndiwo Alevi, analandira motapa pa fuko la Yuda, ndi pa fuko la Simeoni, ndi pa fuko la Benjamini, midzi khumi ndi itatu. Ndipo ana otsala a Kohati analandira molota maere motapa pa mabanja a fuko la Efuremu, ndi pa fuko la Dani, ndi pa fuko la Manase logawika pakati, midzi khumi. Ndipo ana a Geresoni analandira molota maere motapa pa mabanja a fuko la Isakara, ndi pa fuko la Asere, ndi pa fuko la Nafutali, ndi pa fuko la Manase logawika pakati m'Basani, midzi khumi ndi itatu. Ana a Merari, monga mwa mabanja ao, analandira motapa pa fuko la Rubeni, ndi pa fuko la Gadi, ndi pa fuko la Zebuloni midzi khumi ndi iwiri. Motero ana a Israele anapatsa Alevi midzi iyi ndi mabusa ao, molota maere, monga Yehova adalamulira mwa dzanja la Mose. Ndipo anapatsa motapa pa fuko la ana a Yuda, ndi pa fuko la ana a Simeoni, midzi iyi yotchulidwa maina ao; kuti ikhale ya ana a Aroni a mabanja a Akohati, a ana a Levi, pakuti maere oyamba adatulukira iwowa. Ndipo anawapatsa mudzi wa Araba, ndiye atate wa Anaki, womwewo ndi Hebroni, ku mapiri a Yuda, ndi mabusa ake ozungulirapo. Koma minda ya mudzi ndi milaga yake anapatsa Kalebe mwana wa Yefune, ikhale yake. Ndipo kwa ana a Aroni wansembe anapatsa Hebroni ndi mabusa ake, ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzake, ndi Libina ndi mabusa ake; ndi Yatiri ndi mabusa ake, ndi Esitemowa ndi mabusa ake; ndi Holoni ndi mabusa ake, ndi Debiri ndi mabusa ake; ndi Aini ndi mabusa ake, ndi Yuta ndi mabusa ake, ndi Betesemesi ndi mabusa ake; midzi isanu ndi inai yotapira mafuko awiri aja. Ndipo motapira fuko la Benjamini, Gibiyoni ndi mabusa ake, Geba ndi mabusa ake, Anatoti ndi mabusa ake, ndi Alimoni ndi mabusa ake; midzi inai. Midzi yonse ya ana a Aroni, ansembe, ndiyo khumi ndi itatu, ndi mabusa ao. Ndipo mabanja a ana a Kohati, Aleviwo, otsala a ana a Kohati, analandira midzi ya maere ao motapira pa fuko la Efuremu. Ndipo anawapatsa Sekemu ndi mabusa ake ku mapiri a Efuremu, ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzakeyo, ndi Gezere ndi mabusa ake; ndi Kibizaimu ndi mabusa ake, Betehoroni ndi mabusa ake; midzi inai. Ndipo motapira fuko la Dani, Eliteke ndi mabusa ake, ndi Gibetoni ndi mabusa ake; Ayaloni ndi mabusa ake, Gatirimoni ndi mabusa ake; midzi inai. Ndipo motapira pa fuko la Manase logawika pakati, Taanaki ndi mabusa ake, ndi Gatirimoni ndi mabusa ake; midzi iwiri. Midzi yonse ya mabanja a ana otsala a Kohati ndiyo khumi ndi mabusa ao. Ndipo anapatsa ana a Geresoni, a mabanja a Alevi, motapira pa fuko la Manase logawika pakati, Golani m'Basani ndi mabusa ake, ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzakeyo; ndi Beesetera ndi mabusa ake; midzi iwiri. Ndipo motapira pa fuko la Isakara, Kisiyoni ndi mabusa ake, Daberati ndi mabusa ake; Yaramuti ndi mabusa ake, Enganimu ndi mabusa ake; midzi inai. Ndipo motapira pa fuko la Asere, Misala ndi mabusa ake, Abidoni ndi mabusa ake; Helekati ndi mabusa ake, ndi Rehobu ndi mabusa ake; midzi inai. Ndipo motapira pa fuko la Nafutali, Kedesi m'Galileya ndi mabusa ake, ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzakeyo, ndi Hamotidori ndi mabusa ake, ndi Karitani ndi mabusa ake, midzi itatu. Midzi yonse ya Ageresoni monga mwa mabanja ao ndiyo midzi khumi ndi itatu ndi mabusa ao. Ndipo anapatsa kwa mabanja a ana a Merari, otsala a Alevi, motapira pa fuko la Zebuloni, Yokoneamu ndi mabusa ake, ndi Karita ndi mabusa ake, Dimina ndi mabusa ake, Nahalala ndi mabusa ake; midzi inai. Ndipo motapira pa fuko la Rubeni, Bezeri ndi mabusa ake, ndi Yahazi ndi mabusa ake, Kedemoti ndi mabusa ake, ndi Mefaati ndi mabusa ake; midzi inai. Ndipo motapira m'fuko la Gadi, Ramoti m'Giliyadi ndi mabusa ake, ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzakeyo, ndi Mahanaimu ndi mabusa ake; Hesiboni ndi mabusa ake, Yazere ndi mabusa ake: yonse pamodzi midzi inai. Yonseyi ndiyo midzi ya ana a Merari monga mwa mabanja ao, ndiwo otsala a mabanja a Alevi; ndipo gawo lao ndilo midzi khumi ndi iwiri. Midzi yonse ya Alevi, pakati pa cholowa cha ana a Israele ndiyo midzi makumi anai kudza isanu ndi itatu, ndi mabusa ao. Midzi iyi yonse inali nao mabusa ao pozungulira pao: inatero midzi iyi yonse. Motero Yehova anawapatsa Israele dziko lonse adalumbiralo kuwapatsa makolo ao: ndipo analilandira laolao, nakhala m'mwemo. Ndipo Yehova anawapatsa mpumulo pozungulira ponse, monga mwa zonse adalumbirira makolo ao; ndipo pamaso pao sipanaima munthu mmodzi wa adani ao onse; Yehova anapereka adani ao onse m'manja mwao. Sikadasowa kanthu konse ka zinthu zokoma zonse Yehova adazinenera nyumba ya Israele; zidachitika zonse. Pamenepo Yoswa anaitana Arubeni ndi Agadi, ndi fuko la Manase logawika pakati, nanena nao, Mwasunga inu zonsezo anakulamulirani Mose mtumiki wa Yehova; mwamveranso mau anga m'zonse ndinakulamulirani inu; simunasiya abale anu masiku awa ambiri mpaka lero lino, koma mwasunga chisungire lamulo la Yehova Mulungu wanu. Ndipo tsopano Yehova Mulungu wanu wapumitsa abale anu, monga adanena nao; potero bwererani tsopano, mukani ku mahema anu, ku dziko la cholowa chanu chimene Mose mtumiki wa Yehova anakuninkhani tsidya lija la Yordani. Koma samalirani bwino kuti muchite chilangizo ndi chilamulo zimene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulirani, kukonda Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m'njira zake zonse ndi kusunga malamulo ake, ndi kumuumirira Iye, ndi kumtumikira Iye ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse. Momwemo Yoswa anawadalitsa, nawauza amuke; ndipo anamuka ku mahema ao. Ndipo gawo limodzi la fuko la Manase, Mose anawapatsa cholowa m'Basani; koma gawo lina Yoswa anawaninkha cholowa pakati pa abale ao tsidya lija la Yordani kumadzulo. Ndiponso pamene Yoswa anawauza amuke ku mahema ao, anawadalitsa; nanena nao ndi kuti, Bwererani nacho chuma chambiri ku mahema anu, ndi zoweta zambirimbiri, ndi siliva, ndi golide, ndi mkuwa, ndi chitsulo, ndi malaya ambirimbiri; mugawane nao abale anu zofunkha kwa adani anu. Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi fuko la Manase logawika pakati anabwerera, nachoka kwa ana a Israele ku Silo, ndiwo wa m'dziko la Kanani kunka ku dziko la Giliyadi, ku dziko laolao, limene anakhala eni ake, monga mwa lamulo la Yehova, mwa dzanja la Mose. Ndipo pamene anafikira mbali ya ku Yordani, ndilo la m'dziko la Kanani, ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi fuko la Manase logawika pakati anamanga ku Yordani guwa la nsembe, guwa lalikulu maonekedwe ake. Ndipo ana a Israele anamva anthu akuti, Taonani ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi fuko la Manase logawika pakati anamanga guwa la nsembe pandunji pa dziko la Kanani, ku mbali ya ku Yordani, ku mbali ya ana a Israele. Pamene ana a Israele anamva ichi msonkhano wonse wa ana a Israele anasonkhana ku Silo, kuti awakwerere kuwathira nkhondo. Ndipo ana a Israele anatumiza kwa ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi fuko la Manase logawika pakati, ku dziko la Giliyadi, Finehasi mwana wa Eleazara wansembe, ndi akalonga khumi naye; nyumba imodzi ya atate kalonga mmodzi, kotero ndi mafuko onse a Israele; yense wa iwowa ndiye mkulu wa nyumba ya atate ao mwa mabanja a Israele. M'mene anafika kwa ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi fuko la Manase logawika pakati, ku dziko la Giliyadi, ananena nao ndi kuti, Utero msonkhano wonse wa Yehova, Cholakwa ichi nchiyani mwalakwira nacho Mulungu wa Israele, ndi kumtembenukira Yehova lero lino kusamtsatanso, popeza munadzimangira guwa la nsembe kupikisana ndi Yehova lero lino? Kodi mphulupulu ya ku Peori itichipera, imene sitinadziyeretsera mpaka lero lino, ungakhale mliri unadzera msonkhano wa Yehova, kuti mubwerera lero lino kusatsata Yehova? Ndipo kudzakhala kuti popeza lero mupikisana ndi Yehova, mawa adzakwiyira msonkhano wonse wa Israele. Koma mukayesa dziko la cholowa chanu nchodetsa, olokani kulowa m'dziko la cholowa cha Yehova m'mene chihema cha Yehova chikhalamo, nimukhale nacho cholowa pakati pa ife; koma musapikisana ndi Yehova kapena kupikisana nafe, ndi kudzimangira nokha guwa la nsembe, pamodzi ndi guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu. Kodi Akani mwana wa Zera sanalakwe m'choperekedwacho, ndipo mkwiyo unagwera msonkhano wonse wa Israele? Osangoonongeka yekha munthuyo mu mphulupulu yake. Pamenepo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi fuko la Manase logawika pakati anayankha, nanena ndi akulu a mabanja a Israele, Yehova Chauta Mulungu, Yehova Chauta Mulungu, Iye adziwa, ndi Israele adzadziwa; ngati mopikisana, ngati molakwira Yehova, tadzimangira guwa la nsembe, kubwerera kusamtsata Yehova, musatipulumutsa lero lino; kapena ngati kufukizapo nsembe yopsereza, kapena nsembe yaufa, kapena kuperekapo nsembe zoyamika, achifunse Yehova mwini wake; ndipo ngati ife sitinachita ichi chifukwa cha kuopa mlandu, ndi kuti, Masiku akudzawo ana anu akadzanena ndi ana athu, ndi kuti, Muli chiyani inu kwa Yehova Mulungu wa Israele? Pakuti Yehova anaika Yordani ukhale malire pakati pa ife ndi inu, ana a Rubeni, ndi ana a Gadi; mulibe gawo ndi Yehova; motero ana anu adzaleketsa ana athu asaope Yehova. Chifukwa chake tinati, Tiyeni tikonzeretu zotimangira guwa la nsembe, si kufukizapo nsembe yopsereza ai, kapena nsembe yophera ai; koma lidzakhala mboni pakati pa ife ndi inu, ndi pakati pa mibadwo yathu ya m'tsogolo, kuti tikachita ntchito ya Yehova pamaso pake ndi nsembe zathu zopsereza, ndi zophera, ndi zoyamika; kuti ana anu asanene ndi ana athu m'tsogolomo, Mulibe gawo ndi Yehova. Chifukwa chake tinati, Kudzali, akadzatero kwa ife, kapena kwa mibadwo yathu m'tsogolomo, kuti tidzati, Tapenyani, chitsanzo cha guwa la nsembe la Yehova, chomanga makolo athu, si kufukizapo nsembe yopsereza ai, kapena nsembe yophera ai, koma ndilo mboni pakati pa ife ndi inu. Sikungatheke kuti tipikisane ndi Yehova ndi kubwerera lero kusatsata Yehova, kumanga guwa la nsembe la kufukizapo nsembe yopsereza, la nsembe yaufa, kapena yophera, pamodzi ndi guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu lokhala pakhomo pa chihema chake. Pamene Finehasi wansembe, ndi akalonga a msonkhano ndi akulu a mabanja a Israele okhala naye anamva mau adawanena ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi ana a Manase, anawakomera pamaso pao. Ndipo Finehasi, mwana wa Eleazara wansembe ananena ndi ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi ana a Manase, lero lino tidziwa kuti Yehova ali pakati pa ife, pakuti simunalakwira nacho Yehova; tsopano mwalanditsa ana a Israele m'dzanja la Yehova. Ndipo Finehasi mwana wa Eleazara wansembe, ndi akalonga anabwerera kuchokera kwa ana a Rubeni, ndi kwa ana a Gadi, m'dziko la Giliyadi, kudza ku dziko la Kanani kwa ana a Israele, nawabwezera mau. Ndipo mauwo anakomera ana a Israele pamaso pao; ndi ana a Israele analemekeza Mulungu, osanenanso za kuwakwerera ndi kuwathira nkhondo, kuliononga dziko lokhalamo ana a Rubeni ndi ana a Gadi. Ndipo ana a Rubeni ndi ana a Gadi analitcha guwa la nsembelo: Ndilo mboni pakati pa ife kuti Yehova ndiye Mulungu. Ndipo atapita masiku ambiri, Yehova atapumulitsa Israele kwa adani ao onse akuwazungulira, ndipo Yoswa adakalamba nakhala wa zaka zambiri; Yoswa anaitana Aisraele onse, akuluakulu ao, ndi akulu ao, ndi oweruza ao, ndi akapitao ao, nanena nao, Ndakalamba, ndine wa zaka zambiri; ndipo munapenya zonse Yehova Mulungu anachitira mitundu iyi yonse ya anthu chifukwa cha inu; pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye anakuthirirani nkhondo. Taonani, ndakugawirani mitundu ya anthu iyi yotsala ikhale cholowa cha mafuko anu, kuyambira ku Yordani, ndi mitundu yonse ya anthu ndinaipasula, mpaka ku Nyanja Yaikulu ku malowero a dzuwa. Ndipo Yehova Mulungu wanu Iyeyu adzawapirikitsa pamaso panu, ndi kulanda dziko lao kuwachotsa pamaso panu, ndipo mudzalandira dziko lao likhale cholowa chanu; monga Yehova Mulungu wanu ananena ndi inu. Koma mulimbike mtima kwambiri kusunga ndi kuchita zonse zolembedwa m'buku la chilamulo cha Mose, osachipatukira kulamanja kapena kulamanzere; osalowa pakati pa amitundu awa otsala mwa inu; kapena kutchula dzina la milungu yao; osalumbiritsa nalo, kapena kuitumikira, kapena kuigwadira; koma muumirire Yehova Mulungu wanu, monga munachita mpaka lero lino. Pakuti Yehova anaingitsa pamaso panu mitundu yaikulu ndi yamphamvu; koma inu, palibe munthu anaima pamaso panu mpaka lero lino. Munthu mmodzi wa inu adzapirikitsa anthu chikwi chimodzi; pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye amathirira inu nkhondo monga ananena ndi inu. Potero mudzisamalire ndithu kuti mukonde Yehova Mulungu wanu. Koma, mukadzabwerera m'mbuyo pang'ono pokha ndi kuumirira otsala a mitundu awa, ndiwo akutsala pakati pa inu, ndi kukwatitsana nao, ndi kulowana nao, naonso kulowana nanu; dziwani ndithu kuti Yehova Mulungu wanu sadzalandanso dziko la amitundu awa kuwachotsa pamaso panu; koma adzakhala kwa inu deka ndi msampha ndi mkwapulo m'nthiti mwanu, ndi minga m'maso mwanu, mpaka mudzatayika m'dziko lokoma ili anakupatsani Yehova Mulungu wanu. Ndipo taonani, lero lino ndilikumuka njira ya dziko lonse lapansi; ndipo mudziwa m'mitima yanu yonse, ndi m'moyo mwa inu nonse, kuti pa mau okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwe padera mau amodzi; onse anachitikira inu, sanasowepo mau amodzi. Ndipo kudzakhala kuti monga zakugwerani zokoma zonse anakunenerani Yehova Mulungu wanu, momwemo Yehova adzakutengerani zoipa zonse mpaka atakuonongani kukuchotsani m'dziko lokoma ili anakupatsani Yehova Mulungu wanu. Mukalakwira chipangano cha Yehova Mulungu wanu chimene analamulira inu ndi kumuka ndi kutumikira milungu ina ndi kuigwadira, mkwiyo wa Mulungu udzayakira inu, nimudzatayika msanga m'dziko lokomali anakupatsani. Ndipo Yoswa anasonkhanitsa mafuko onse a Israele ku Sekemu, naitana akuluakulu a Israele ndi akulu ao, ndi oweruza ao, ndi akapitao ao; ndipo anadzilangiza pamaso pa Mulungu. Ndipo Yoswa ananena ndi anthu onse, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Kale lija makolo anu anakhala tsidya lija la mtsinje, ndiye Tera, atate wa Abrahamu ndi atate wa Nahori; natumikira milungu ina iwowa. Ndipo ndinamtenga kholo lanu Abrahamu tsidya lija la mtsinje, ndi kumuyendetsa m'dziko lonse la Kanani ndi kuchulukitsa mbeu zake ndi kumpatsa Isaki. Ndi kwa Isaki ndinapatsa Yakobo ndi Esau, ndipo ndinampatsa Esau phiri la Seiri likhale lakelake; koma Yakobo ndi ana ake anatsikira kunka ku Ejipito. Pamenepo ndinatuma Mose ndi Aroni, ndipo ndinasautsa Aejipito, monga ndinachita pakati pake; ndipo nditatero ndinakutulutsani. Ndipo ndinatulutsa atate anu m'Ejipito; ndipo munadza kunyanja; koma Aejipito analondola atate anu ndi magaleta ndi apakavalo mpaka ku Nyanja Yofiira. Ndipo pamene anafuula kwa Yehova, anaika mdima pakati pa inu ndi Aejipito nawatengera nyanja, nawamiza; ndi maso anu anapenya chochita Ine m'Ejipito; ndipo munakhala m'chipululu masiku ambiri. Pamenepo ndinakulowetsani inu m'dziko la Aamori okhala tsidya lija la Yordani; nagwirana nanu iwowa; ndipo ndinawapereka m'dzanja lanu, nimunalandira dziko lao likhale lanulanu; ndipo ndinawaononga pamaso panu. Pamenepo Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu, anauka naponyana ndi Israele; natuma naitana Balamu mwana wa Beori atemberere inu; koma sindinafuna kumvera Balamu, potero anakudalitsani chidalitsire, ndipo ndinakulanditsani m'dzanja lake. Pamenepo munaoloka Yordani, ndi kufika ku Yeriko; ndi eni ake a ku Yeriko anaponyana nanu nkhondo, Aamori, ndi Aperizi, ndi Akanani, ndi Ahiti, ndi Agirigasi, Ahivi, ndi Ayebusi; ndipo ndinawapereka m'dzanja lanu. Ndipo ndinatuma mavu atsogolere inu, amene anawaingitsa pamaso panu, ndiwo mafumu awiri a Aamori; osati ndi lupanga lako, kapena ndi uta wako ai. Ndipo ndinakupatsani dziko limene simunagwiramo ntchito, ndi midzi simunaimanga, ndipo mukhala m'mwemo; mukudya za m'minda yamphesa, ndi minda ya azitona imene simunaioka. Ndipo tsopano, opani Yehova ndi kumtumikira ndi mtima wangwiro ndi woona; nimuchotse milungu imene makolo anu anaitumikira tsidya lija la mtsinje, ndi m'Ejipito; nimutumikire Yehova. Ndipo ngati kutumikira Yehova kukuipirani mudzisankhire lero amene mudzamtumikira, kapena milungu imene anaitumikira makolo anu okhala tsidya lija la mtsinje, kapena milungu ya Aamori amene mukhala m'dziko lao; koma ine, ndi a m'nyumba yanga, tidzatumikira Yehova. Ndipo anthu anayankha, nati, Sikungatheke kuti timsiye Yehova, ndi kutumikira milungu ina; pakuti Yehova Mulungu wathu ndi Iye amene anatikweza kutitulutsa m'dziko la Ejipito kunyumba ya akapolo, nachita zodabwitsa zazikuluzo pamaso pathu, natisunga m'njira monse tidayendamo, ndi pakati pa anthu onse amene tinapita pakati pao; ndipo Yehova anaingitsa pamaso pathu anthu awa onse, ngakhale Aamori okhala m'dzikomo; chifukwa chake ifenso tidzatumikira Yehova, pakuti ndiye Mulungu wathu. Ndipo Yoswa anati kwa anthu, Simukhoza inu kutumikira Yehova pakuti ndiye Mulungu woyera, ndi Mulungu wansanje; sadzalekerera zolakwa zanu, kapena zochimwa zanu. Mukasiya Yehova, ndi kutumikira milungu yachilendo, adzatembenuka ndi kukuchitirani choipa, ndi kukuthani, angakhale anakuchitirani chokoma. Ndipo anthu anati kwa Yoswa, Iaitu, koma tidzatumikira Yehova. Ndipo Yoswa ananena ndi anthu, Inu mwadzichitira mboni inu nokha kuti mwadzisankhira Yehova kumtumikira Iye. Ndipo anati, Ndife mboni. Ndipo tsopano, chotsani milungu yachilendo ili pakati pa inu, ndi kulozetsa mitima yanu kwa Yehova, Mulungu wa Israele. Ndipo anthu anati kwa Yoswa, Tidzamtumikira Yehova Mulungu wathu ndi kumvera mau ake. Motero Yoswa anachita pangano ndi anthu tsiku lija, nawaikira lemba ndi chiweruzo m'Sekemu. Ndipo Yoswa analembera mau awa m'buku la chilamulo cha Mulungu; natenga mwala waukulu, nauimitsa apo patsinde pa thundu wokhala pa malo opatulika a Yehova. Ndipo Yoswa anati kwa anthu onse, Taonani, mwala uwu udzakhala mboni yotitsutsa; pakuti udamva mau onse a Yehova amene ananena kwa ife; ndipo udzakhala mboni yotsutsa inu, mungakanize Mulungu wanu. Pamenepo Yoswa anauza anthu amuke, yense ku cholowa chake. Ndipo kunali, zitatha izi, Yoswa mwana wa Nuni mtumiki wa Yehova, adafa, wa zaka zana ndi khumi. Ndipo anamuika m'malire a cholowa chake m'Timnati-Sera, ndiwo ku mapiri a Efuremu kumpoto kwa phiri la Gaasi. Ndipo Israele anatumikira Yehova masiku onse a Yoswa, ndi masiku onse a akuluakulu otsala atafa Yoswa, amene anadziwa ntchito yonse ya Yehova anaichitira Israele. Ndipo mafupa a Yosefe amene ana a Israele anakwera nao kuchokera ku Ejipito anawaika ku Sekemu, pa kadziko kamene adakagula Yakobo kwa ana a Hamori atate wa Sekemu ndi kuwapatsa ndalama zana; ndipo anakhala cholowa cha ana a Yosefe. Eleazaranso mwana wa Aroni anafa; ndipo anamuika pa phiri la Finehasi mwana wake, limene adampatsa ku mapiri a Efuremu. Ndipo atafa Yoswa, ana a Israele anafunsira kwa Yehova ndi kuti, Adzayamba ndani kutikwerera pa Akanani kuwathira nkhondo? Ndipo Yehova anati, Akwere Yuda; taonani, ndapereka dzikoli m'dzanja lake. Ndipo Yuda ananena ndi Simeoni mkulu wake, Kwera nane ku gawo langa kuti tiwathire nkhondo Akanani; ndipo inenso ndidzamuka nawe ku gawo lako. Namuka naye Simeoni. Ndipo Yuda atakwera, Yehova anapereka Akanani ndi Aperizi m'dzanja lao, ndipo anakantha a iwowa anthu zikwi khumi ku Bezeki. Ndipo anapeza Adoni-Bezeki m'Bezeki, namthira nkhondo nakantha Akanani ndi Aperizi. Koma Adoni-Bezeki anathawa; ndipo anampirikitsa, namgwira, namdula zala zazikulu za m'manja ndi za m'mapazi. Pamenepo anati Adoni-Bezeki, Mafumu makumi asanu ndi awiri odulidwa zala zazikulu za m'manja ndi m'mapazi anaola kakudya kao pansi pa gome panga; monga ndinachita ine, momwemo Mulungu wandibwezera. Ndipo anadza naye ku Yerusalemu, nafa iye komweko. Ndipo ana a Yuda anachita nkhondo pa Yerusalemu, naulanda, naukantha ndi lupanga lakuthwa, natentha mudzi ndi moto. Ndipo atatero ana a Yuda anatsika kuthirana nao nkhondo Akanani akukhala kumapiri, ndi kumwera ndi kuchidikha. Ndipo Yuda anamuka kwa Akanani akukhala m'Hebroni; koma kale dzina la Hebroni ndilo mudzi wa Ariba; ndipo anakantha Sesai, ndi Ahimani, ndi Talimai. Pochoka pamenepo anamuka kwa nzika za ku Debiri, koma kale dzina la Debiri ndilo mudzi wa Kiriyati-Sefere. Ndipo Kalebe anati, Iye amene akantha mudzi wa Kiriyati-Sefere, naulanda, yemweyo ndidzampatsa Akisa mwana wanga wamkazi akhale mkazi wake. Ndipo Otiniyele, mwana wa Kenazi mng'ono wa Kalebe anaulanda, ndipo anampatsa Akisa mwana wake wamkazi akhale mkazi wake. Ndipo kunali, m'mene anamdzera, anamkakamiza mwamuna wake kuti apemphe atate wake ampatse munda; natsika pa bulu wake; ndipo Kalebe ananena naye, Ufunanji? Ndipo anati kwa iye, Mundipatse dalitso; popeza mwandipatsa dziko la kumwera, ndipatsenso zitsime za madzi. Pamenepo Kalebe anampatsa zitsime za kumtunda ndi zitsime za kunsi. Ndipo ana a Mkeni mlamu wake wa Mose, anakwera kutuluka m'mudzi wa m'migwalangwa pamodzi ndi ana a Yuda, nalowa m'chipululu cha Yuda chokhala kumwera kwa Aradi; namuka iwo nakhala ndi anthuwo. Ndipo Yuda anamuka ndi Simeoni mkulu wake, nakantha Akanani akukhala m'Zefati, nauononga konse. Koma dzina la mudziwo analitcha Horoma. Yuda analandanso Gaza ndi malire ake, ndi Asikeloni ndi malire ake ndi Ekeroni ndi malire ake. Ndipo Yehova anali ndi Yuda, iye nawaingitsa a kumapiri, osaingitsa nzika za kuchigwa, popeza zinali nao magaleta achitsulo. Ndipo anapatsa Kalebe Hebroni monga Mose adanena; iye nawaingitsa komweko ana amuna atatu a Anaki. Koma ana a Benjamini sanaingitse Ayebusi okhala m'Yerusalemu; koma Ayebusi anakhala m'Yerusalemu pamodzi ndi ana a Benjamini, mpaka lero lino. Ndipo anakwera iwo a m'nyumba ya Yosefe, naonso kunka ku Betele; ndipo Yehova anakhala nao. Ndipo iwo a m'nyumba ya Yosefe anatumiza ozonda ku Betele. Koma kale dzina la mudziwo ndilo Luzi. Ndipo alonda anaona munthu alikutuluka m'mudzi, nanena naye, Utionetsetu polowera m'mudzi, ndipo tidzakuchitira chifundo. Nawaonetsa polowera m'mudzi iye, naukantha mudzi iwowa ndi lupanga lakuthwa; koma analola munthuyo ndi banja lake lonse amuke. Ndipo munthuyo anamuka ku dziko la Ahiti, namanga mudzi, nautcha dzina lake Luzi; ndilo dzina lake mpaka lero lino. Koma Manase sanaingitse a ku Beteseani ndi midzi yake kapena a Taanaki ndi midzi yake, kapena nzika za ku Dori ndi midzi yake, kapena nzika za ku Ibleamu ndi midzi yake, kapena nzika za ku Megido ndi midzi yake; koma Akanani anakhumba kukhala m'dziko muja. Ndipo kunali, atakula mphamvu Israele, anasonkhetsa Akanani, osawaingitsa onse. Ndipo Efuremu sanaingitse Akanani okhala m'Gezere; koma Akanani anakhala m'Gezere pakati pao. Zebuloni sanaingitse nzika za ku Kitironi, kapena za ku Nahaloli; koma Akanani anakhala pakati pao, nawasonkhera. Asere sanaingitse nzika za ku Ako, kapena nzika za ku Sidoni, kapena a Alabu, kapena a Akizibu, kapena a Heliba, kapena a Afiki, kapena a Rehobu; koma Asere anakhala pakati pa Akanani nzika za kudziko; pakuti sanawaingitse. Nafutali sanaingitse nzika za ku Betesemesi, kapena nzika za ku Betanati; koma anakhala pakati pa Akanani, nzika za kudziko; koma nzika za ku Betesemesi, ndi a ku Betanati zinawasonkhera. Ndipo Aamori anakankha ana a Dani akhale kumapiri pakuti sanawalole atsikire kuchigwa; Aamori anakhumbanso kukhala kuphiri la Heresi, ku Ayaloni, ndi ku Saalibimu; koma dzanja la a m'nyumba ya Yosefe linawalaka, nakhala iwo akupereka msonkho. Ndipo malire a Aamori anayambira pokwerera pa Akarabimu, pathanthwe ku Sela, ndi pokwererapo. Ndipo mthenga wa Yehova anakwera kuchokera ku Giligala kunka ku Bokimu. Ndipo anati, Ndinakukweretsani kuchokera ku Ejipito, ndi kulowetsa inu m'dziko limene ndinalumbirira makolo anu; ndipo ndinati, Sindidzathyola chipangano changa nanu ku nthawi yonse; ndipo inu, musamachita pangano ndi nzika za m'dziko ili; muzigamula maguwa ao a nsembe. Koma simunamvera mau anga; mwachichita ichi chifukwa ninji? Chifukwa chakenso ndinati, Sindidzawapirikitsa kuwachotsa pamaso panu; koma adzakhala ngati minga m'nthiti zanu, ndi milungu yao idzakhalira inu msampha. Ndipo kunali, pamene mthenga wa Yehova ananena mau awa kwa ana onse a Israele, anthuwo anakweza mau ao, nalira misozi. Potero analitcha dzina la malowo Bokimu: namphera Yehova nsembe pomwepo. Pamene Yoswa atawalola anthu amuke, ana a Israele anamuka, yense ku cholowa chake, dziko likhale laolao. Ndipo anthuwo anatumikira Yehova masiku onse a Yoswa, ndi masiku onse a akuluakulu otsala atafa Yoswa, amene adaona ntchito yaikulu yonse ya Yehova anaichitira Israele. Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Yehova anafa wa zaka zake zana ndi khumi. Ndipo anamuika m'malire a cholowa chake m'Timnati-Heresi, ku mapiri a Efuremu, kumpoto kwa phiri la Gaasi. Ndiponso mbadwo uwu wonse unasonkhanidwa kuikidwa kwa makolo ao; nuuka mbadwo wina pambuyo pao; wosadziwa Yehova kapena ntchitoyi adaichitira Israele. Ndipo ana a Israele anachita choipa pamaso pa Yehova, natumikira Abaala; nasiya Yehova Mulungu wa makolo ao, amene adawatulutsa m'dziko la Ejipito, natsata milungu ina, milungu ya mitundu ya anthu okhala pozungulira pao, naigwadira; nautsa mkwiyo wa Yehova. Ndipo anasiya Yehova, natumikira Baala ndi Asitaroti. Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele, ndipo anawapereka m'manja a ofunkha kuti awafunkhe; nawagulitsa m'dzanja la adani ao akuwazungulira osakhozanso iwowo kuima pamaso pa adani ao. Kuli konse anatuluka, dzanja la Yehova linawakhalira moipa, monga Yehova adanena, ndi monga Yehova adawalumbirira; nasautsika kwambiri iwowa. Ndipo Yehova anautsa oweruza, amene anawapulumutsa m'dzanja la iwo akuwafunkha. Koma sanamvere angakhale oweruza ao, pakuti anamuka kupembedza milungu ina, naigwadira; anapatuka msanga m'njira yoyendamo makolo ao, pomvera malamulo a Yehova; sanatero iwowa. Ndipo pamene Yehova anawaukitsira oweruza, Yehova anakhala naye woweruzayo, nawapulumutsa m'dzanja la adani ao masiku onse a woweruzayo; pakuti Yehova anagwidwa chisoni pa kubuula kwao chifukwa cha iwo akuwapsinja ndi kuwatsendereza. Koma kunali atafa woweruzayo anabwerera m'mbuyo, naposa makolo ao ndi kuchita moipitsa, ndi kutsata milungu ina kuitumikira ndi kuigwadira, sanaleke kanthu ka machitidwe ao kapena ka njira yao yatcheni. Ndipo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele; nati Iye, Popeza mtundu uwu unalakwira chipangano changa chimene ndinalamulira makolo ao, osamvera mau anga; Inenso sindionjeza kuingitsa pamaso pao a mitundu ina imene Yoswa adaisiya pakufa iyeyu; kuti ndiyese nayo Israele ngati adzasunga njira ya Yehova kuyendamo monga anaisunga makolo ao, kapena iai. Motero Yehova analeka mitundu iyi osaiingitsa msanga, ndipo sadaipereka m'dzanja la Yoswa. Ndipo iyo ndiyo mitundu ya anthu anaisiyapo Yehova kuyesa nayo Israele, ndiwo onse amene sanadziwe nkhondo zonse za Kanani; chifukwa chake ndicho chokha chakuti adziwitse mibadwo ya ana a Israele ndi kuwaphunzitsa nkhondo, ngakhale iwo okhaokha osaidziwa konse kale; anasiya mafumu asanu a Afilisti ndi Akanani onse, ndi Asidoni, ndi Ahivi okhala m'phiri la Lebanoni, kuyambira phiri la Baala-Heremoni mpaka polowera ku Hamati. Amenewo anakhala choyesera Israele kuti Yehova adziwe ngati adzamvere malamulo ake, amene analamulira makolo ao mwa dzanja la Mose. Ndipo ana a Israele anakhala pakati pa Akanani, Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi; nakwatira ana akazi a iwowa, napereka ana ao akazi kwa ana amuna a iwowa natumikira milungu yao. Ndipo ana a Israele anachita choipa pamaso pa Yehova, naiwala Yehova Mulungu wao, natumikira Abaala ndi zifanizo. Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele ndipo anawagulitsa m'dzanja la Kusani-Risataimu, mfumu ya Mesopotamiya; ndi ana a Israele anatumikira Kusani-Risataimu zaka zisanu ndi zitatu. Ndipo pamene ana a Israele anafuula kwa Yehova, Yehova anaukitsira ana a Israele mpulumutsi amene anawapulumutsa, ndiye Otiniyele mwana wa Kenazi, mng'ono wake wa Kalebe. Ndipo unamdzera mzimu wa Yehova, iye naweruza Israele, natuluka kunkhondo; napereka Yehova Kusani-Risataimu mfumu ya Mesopotamiya m'dzanja lake; ndi dzanja lake linamlaka Kusani-Risataimu. Pamenepo dziko linapumula zaka makumi anai; ndi Otiniyele mwana wa Kenazi anafa. Koma ana a Israele anaonjezanso kuchita choipa pamaso pa Yehova; pamenepo Yehova analimbitsa Egiloni mfumu ya Mowabu pa Israele, popeza anachita choipa pamaso pa Yehova. Ndipo anadzisonkhanitsira ana a Amoni ndi a Amaleke, namuka nakantha Israele, nalanda mudzi wa m'migwalangwa nakhalamo. Ndipo ana a Israele anatumikira Egiloni mfumu ya Mowabu zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu. Koma pamene ana a Israele anafuula kwa Yehova, Yehova anawaukitsira mpulumutsi, Ehudi mwana wa Gera, Mbenjamini, munthu wamanzere, ndipo ana a Israele anatumiza mtulo m'dzanja lake kwa Egiloni mfumu ya Mowabu. Ndipo Ehudi anadzisulira lupanga lakuthwa konsekonse utali wake mkono; nalimangirira pansi pa zovala zake pa ntchafu ya kulamanja. Ndipo anapereka mtulo kwa Egiloni, mfumu ya Mowabu; koma Egiloni ndiye munthu wonenepa ndithu. Ndipo atatha kupereka mtulowo, anauza anthu onyamula mtulo achoke. Koma iye mwini anabwerera pa mafano osema ali ku Giligala, nati, Ndili nao mau achinsinsi kwa inu, mfumu. Nati iye, Khalani chete. Ndipo anatuluka onse akuimapo. Ndipo Ehudi anamdzera alikukhala pa yekha m'chipinda chosanja chopitidwa mphepo. Nati Ehudi, Ndili nao mau a Mulungu akukuuzani. Nauka iye pa mpando wake. Ndipo Ehudi anatulutsa dzanja lake lamanzere nagwira lupanga ku ntchafu ya kulamanja nampyoza m'mimba mwake; ndi chigumbu chake chinalowa kutsata mpeni wake; ndi mafuta anaphimba mpeniwo, pakuti sanasolole lupanga m'mimba mwake; nilituluka kumbuyo. Pamenepo Ehudi anatuluka kukhonde namtsekera pamakomo pa chipinda chosanja nafungulira. Ndipo atatuluka iye, anadza akapolo ake; napenya, ndipo taonani pamakomo pa chipinda chosanja mpofungulira; nati iwo, Angophimba mapazi m'chipinda chake chosanja chopitidwa mphepo. Ndipo analindirira mpaka anachita manyazi; koma taonani, sanatsegule pamakomo pa chipinda chosanja. Pamenepo anatenga mfungulo natsegula; ndipo taonani, mbuye wao wagwa pansi, wafa. Ndipo Ehudi anapulumuka pakuchedwa iwo, napitirira pa mafano osema, napulumuka kufikira Seira. Ndipo kunali, pakufika iye anaomba lipenga ku mapiri a Efuremu; ndi ana a Israele anatsika naye kuchokera kumapiri, nawatsogolera iye. Ndipo ananena nao, Nditsateni ine, pakuti Yehova wapereka adani anu Amowabu m'manja mwanu. Ndipo anatsika ndi kumtsata, natsekereza Amowabu madooko a Yordani, osalola mmodzi aoloke. Ndipo anakantha Amowabu nyengo ija anthu zikwi khumi, onsewa anthu amoyo, ndi ngwazi; ndipo sanapulumuke ndi mmodzi yense. Motero anagonjetsa Mowabu tsiku lija pansi pa dzanja la Israele. Ndipo dziko linapumula zaka makumi asanu ndi atatu. Atapita iye kunali Samigara, mwana wa Anati amene anakantha Afilisti mazana asanu ndi limodzi ndi mtoso wa ng'ombe; nayenso anapulumutsa Israele. Ndipo ana a Israele anaonjeza kuchita choipa pamaso pa Yehova, atafa Ehudi. Ndipo Yehova anawagulitsa m'dzanja la Yabini mfumu ya Kanani, wochita ufumu ku Hazori; kazembe wake wa nkhondo ndiye Sisera, wokhala ku Haroseti wa amitundu. Ndipo ana a Israele anafuula kwa Yehova; pakuti anali nao magaleta achitsulo mazana asanu ndi anai; napsinja ana a Israele kolimba zaka makumi awiri. Ndipo Debora, mneneri wamkazi, ndiye mkazi wake wa Lapidoti, anaweruza Israele nyengo ija. Ndipo anakhala patsinde pa mgwalangwa wa Debora pakati pa Rama ndi Betele ku mapiri a Efuremu; ndi ana a Israele anakwera kwa iye awaweruze. Ndipo anatuma, naitana Baraki mwana wa Abinowamu, achoke m'Kedesi-Nafutali; nanena naye, Kodi Yehova Mulungu wa Israele sanalamulire ndi kuti, Muka, nulunjike kuphiri la Tabori, nuwatenge, apite nawe anthu zikwi khumi a ana a Nafutali ndi ana a Zebuloni? Ndipo ndidzamkoka Sisera, kazembe wa nkhondo ya Yabini, akudzere ku mtsinje wa Kisoni, ndi magaleta ake, ndi aunyinji ake; ndipo ndidzampereka m'dzanja lako. Ndipo Baraki anati kwa iye, Ukamuka nane, ndidzamuka; ukapanda kumuka nane, sindimuka. Nati iye, Kumuka ndidzamuka nawe, koma ulendo umukawo, sudzachita nao ulemu; pakuti Yehova adzagulitsa Sisera m'dzanja la mkazi. Motero Debora anauka namuka ndi Baraki ku Kedesi. Ndipo Baraki anaitana Zebuloni ndi Nafutali asonkhane ku Kedesi; iye nakwera ndi anthu zikwi khumi akumtsata; Deboranso anakwera kunka naye. Ndipo Hebere Mkeni anadzisiyanitsa ndi Akeni, ndi ana a Hobabu mlamu wake wa Mose, namanga mahema ake mpaka thundu wa m'Zaananimu, ndiwo wa ku Kedesi. Ndipo anauza Sisera kuti Baraki mwana wa Abinowamu wakwera kuphiri la Tabori. Pamenepo Sisera anasonkhanitsa magaleta ake onse ndiwo magaleta mazana asanu ndi anai achitsulo, ndi anthu onse okhala naye, kuyambira Haroseti wa amitundu mpaka mtsinje wa Kisoni. Ndipo Debora anati kwa Baraki, Nyamuka; pakuti ili ndi tsikuli Yehova wapereka Sisera m'dzanja lako; sanatuluke kodi Yehova pamaso pako? Potero Baraki anatsika kuphiri la Tabori ndi amuna zikwi khumi akumtsata. Ndipo Ambuye anaononga Sisera ndi magaleta onse ndi gulu lankhondo lonse, ndi lupanga lakuthwa pamaso pa Baraki; koma Sisera anatsika pagaleta nathawa choyenda pansi. Koma Baraki anatsata magaleta ndi gululo mpaka Haroseti wa amitundu; ndi gulu lonse lankhondo la Sisera linagwa ndi lupanga lakuthwa, sanatsale munthu ndi mmodzi yense. Koma Sisera anathawira choyenda pansi ku hema wa Yaele mkazi wa Hebere Mkeni; pakuti panali mtendere pakati pa Yabini mfumu ya Hazori, ndi nyumba ya Hebere Mkeni. Ndipo Yaele anatuluka kukomana ndi Sisera, nanena naye, Patuka, mbuye wanga, patukira kwa ine kuno; usaope. Ndipo anapatukira kwa iye kulowa m'hema, namfunda ndi chimbwi. Pamenepo ananena naye, Ndipatsetu madzi pang'ono ndimwe; popeza ndine waludzu. Ndipo anatsegula thumba la mkaka, nampatsa amwe, namfunda. Ndipo Sisera ananena naye, Taima pakhomo pa hema, ndipo kudzali, akadza munthu, akakufunsa akati, Pali munthu pano kodi? Uziti, Palibe. Pamenepo Yaele mkazi wa Hebere anatenga chichiri cha hema, natenga nyundo m'dzanja lake namdzera monyang'ama, nakhomera chichiri chilowe m'litsipa mwake; nichinapyoza kulowa m'nthaka; popeza anali m'tulo tofa nato ndi kulema; nafa. Ndipo taonani, pomlondola Sisera Barakiyo, Yaele anatuluka kukomana naye, nati kwa iye, Idza kuno, ndidzakuonetsa munthu umfunayo. Potero anamdzera, ndipo taonani, Sisera wagwa, wafa, ndi chichiri m'litsipa mwake. Momwemo Mulungu anagonjetsa tsiku lija Yabini mfumu ya Kanani pamaso pa ana a Israele. Ndipo dzanja la ana a Israele linamkabe ndi kulimbika pa Yabini mfumu ya Kanani mpaka adamuononga Yabini mfumu ya Kanani. Ndipo Debora ndi Baraki mwana wa Abinowamu anaimba tsiku lomwelo ndi kuti, Lemekezani Yehova pakuti atsogoleri m'Israele anatsogolera, pakuti anthu anadzipereka mwaufulu. Imvani mafumu inu; tcherani makutu, akalonga inu; ndidzamuimbira ine Yehova, inetu; ndidzamuimbira nyimbo, Yehova, Mulungu wa Israele. Yehova, muja mudatuluka m'Seiri, muja mudayenda kuchokera ku thengo la Edomu, dziko linanjenjemera, thambo lomwe linakha, inde mitambo inakha madzi. Mapiri anagwedezeka pamaso pa Yehova, Sinai lili pamaso pa Yehova, Mulungu wa Israele. Masiku a Samigara, mwana wa Anati, masiku a Yaele maulendo adalekeka ndi apanjira anayenda mopazapaza. Milaga idalekeka m'Israele, idalekeka. Mpaka ndinauka ine Debora, ndinauka ine amai wa Israele. Anasankha milungu yatsopano, pamenepo nkhondo inaoneka kuzipata. Ngati chikopa kapena nthungo zidaoneka mwa zikwi makumi anai a Israele? Mtima wanga uvomerezana nao olamulira a m'Israele, amene anadzipereka mwaufulu mwa anthu. Lemekezani Yehova. Inu akuyenda okwera pa abulu oyera, inu akukhala poweruzira, ndi inu akuyenda m'njira, fotokozerani. Posamveka phokoso la amauta potunga madzi, pomwepo adzafotokozera zolungama anazichita Yehova, zolungama anazichita m'milaga yake, m'Israele. Pamenepo anthu a Yehova anatsikira kuzipata. Galamuka, Debora, galamuka, galamuka, galamuka, unene nyimbo; uka, Baraki, manga nsinga ndende zako, mwana wa Abinowamu, iwe. Pamenepo omveka otsala anatsika ndi anthu; Yehova ananditsikira pakati pa achamuna. Anafika Aefuremu amene adika mizu m'Amaleke; Benjamini anakutsata iwe pakati pa anthu ako. Ku Makiri kudachokera olamulira, ndi ku Zebuloni iwo akutenga ndodo ya mtsogoleri. Akalonga a Isakara anali ndi Debora; monga Isakara momwemo Baraki, anawatuma m'chigwa namka choyenda pansi. Pa mitsinje ya Rubeni panali zotsimikiza mtima zazikulu. Wakhaliranji pakati pa makola, kumvera kulira kwa zoweta? Ku timitsinje ta Rubeni kunali zotsimikiza mtima zazikulu. Giliyadi anakhala tsidya lija la Yordani; ndi Dani, akhaliranji m'zombo? Asere anakhala pansi m'mphepete mwa nyanja, nakhalitsa pa nyondo yake ya nyanja. Zebuloni ndiwo anthu anataya moyo wao mpaka imfa, Nafutali yemwe poponyana pamisanje. Anadza mafumu nathira nkhondo; pamenepo anathira nkhondo mafumu a Kanani. M'Taanaki, ku madzi a Megido; osatengako phindu la ndalama. Nyenyezi zinathira nkhondo yochokera kumwamba, m'mipita mwao zinathirana ndi Sisera. Mtsinje wa Kisoni unawakokolola, mtsinje uja wakale, mtsinje wa Kisoni. Yenda mwamphamvu, moyo wangawe. Pamenepo ziboda za akavalo zinaguguda. Ndi kutumphatumpha, kutumphatumpha kwa anthu ake eni mphamvu. Mutemberere Merozi, ati mthenga wa Yehova, mutemberere chitemberere nzika zake; pakuti sanadzathandize Yehova, kumthandiza Yehova pa achamuna. Wodalitsika, woposa akazi, akhale Yaele mkazi wa Hebere Mkeni. Akhale wodalitsika woposa akazi a m'hema. Mwamunayo anapempha madzi, anampatsa mkaka, anamtengera mafuta a mkaka m'chotengera cha mfulu. Dzanja lake analitambasulira kuchichiri, ndi dzanja lake lamanja ku nyundo ya antchito, nakhomera Sisera, nakantha mutu wake, inde, anaphwanya napyoza m'litsipa mwake. Pa mapazi ake anabzong'onyoka, anagwa, anagona; pa mapazi ake anabzong'onyoka, anagwa; pobzong'onyokapo, pamenepo wagwa wafa. Anapenyerera ali pazenera, nafuula Make wa Sisera, pa sefa wake, achedweranji galeta wake? Zizengerezeranji njinga za magaleta ake? Akazi anzake omveka anzeru anamyankha; koma anadziyankhira yekha mau. Kodi sanapeze, sanagawe zofunkha? Namwali, anamwali awiri kwa munthu aliyense. Chofunkha cha nsalu za mawangamawanga kwa Sisera; chofunkha cha nsalu za mawangamawanga, za maluwa, nsalu za mawangamawanga, za maluwa konsekonse, kwa chofunkha cha khosi lake. Adani anu onse, Yehova, atayike momwemo. Koma iwo akukonda Inu akhale ngati dzuwa lotuluka mu mphamvu yake. Ndipo dziko linapumula zaka makumi anai. Koma ana a Israele anachita choipa pamaso pa Yehova; ndipo Yehova anawapereka m'dzanja la Midiyani zaka zisanu ndi ziwiri. Pamene dzanja la Midiyani linalaka Israele, ana a Israele anadzikonzera ming'ang'ala ya m'mapiri, ndi mapanga, ndi malinga chifukwa cha Midiyani. Ndipo kunali, akabzala Israele, amakwera Amidiyani, ndi Amaleke, ndi ana a kum'mawa, inde amawakwerera; nawamangira misasa, namaononga zipatso za m'dziko mpaka ufika ku Gaza, osawasiyira chochirira njala m'Israele, ngakhale nkhosa, kapena ng'ombe, kapena bulu. Pakuti anakwera nazo zoweta zao ndi mahema ao, analowa ngati dzombe kuchuluka kwao; iwowa ndi ngamira zao zomwe nzosawerengeka; ndipo analowa m'dziko kuliononga. Ndipo Israele anafooka kwambiri chifukwa cha Midiyani; ndipo ana a Israele anafuula kwa Yehova. Ndipo kunali, pamene ana a Israele anafuula kwa Yehova chifukwa cha Midiyani, Yehova anatuma munthu mneneri kwa ana a Israele, nanena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Ine ndinakukwezani kuchokera m'Ejipito, ndi kukutulutsani m'nyumba ya ukapolo; ndipo ndinakulanditsani m'dzanja la Aejipito, ndi m'dzanja la onse akupsinja inu, ndi kuwaingitsa pamaso panu, ndi kukupatsani dziko lao; ndipo ndinati kwa inu, Ine ndine Yehova Mulungu wanu; musamaopa milungu ya Aamori amene mukhala m'dziko lao; koma simunamvera mau anga. Pamenepo anadza mthenga wa Yehova, nakhala patsinde pa thundu wokhala m'Ofura, wa Yowasi Mwabiyezere; ndi mwana wake Gideoni analikuomba tirigu m'mopondera mphesa, awabisire Amidiyani. Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera, nati kwa iye, Yehova ali nawe, ngwazi iwe, wamphamvu iwe. Ndipo Gideoni ananena naye, Mbuye wanga, ngati Yehova ali nafe chatigwera ife bwanji chonsechi? Ndipo zili kuti zodabwitsa zake zonse zimene makolo athu anatiwerengera, ndi kuti, Sanatikweze kodi Yehova kuchokera m'Ejipito? Koma tsopano Yehova watitaya natipereka m'dzanja la Midiyani. Pamenepo Yehova anamtembenukira, nati, Muka nayo mphamvu yako iyi, nupulumutse Israele m'dzanja la Midiyani. Sindinakutuma ndi Ine kodi? Ndipo anati kwa Iye, Ha! Mbuye, ndidzapulumutsa Israele ndi chiyani? Taonani, banja langa lili loluluka m'Manase, ndipo ine ndine wamng'ono m'nyumba ya atate wanga. Ndipo Yehova ananena naye, Popeza Ine ndidzakhala nawe udzakantha Amidiyani ngati munthu mmodzi. Ndipo anati kwa Iye, Ngati mundikomera mtima mundionetse chizindikiro tsopano chakuti ndi Inu wakunena nane. Musachoke pano, ndikupemphani, mpaka ndikudzerani ndi kutulutsa chopereka changa ndi kuchiika pamaso panu. Ndipo anati, Ndidzalinda mpaka ubwera. Ndipo Gideoni analowa, nakonza kambuzi ndi mikate yopanda chotupitsa ya efa wa ufa; nyamayi anaiika m'lichero, ndi msuzi anauthira mumbale, natuluka nazo kwa Iye ali patsinde pa thundu, nazipereka. Koma mthenga wa Mulungu ananena naye, Tenga nyamayi ndi mikate yopanda chotupitsa ndi kuziika pathanthwe pano ndi kutsanula msuzi. Ndipo anatero. Pamenepo mthenga wa Yehova anatambasula nsonga ya ndodo inali m'dzanja lake, nakhudza nyamayi ndi mikate yopanda chotupitsa; ndipo unatuluka moto m'thanthwe nunyeketsa nyama ndi mikate yopanda chotupitsa; ndi mthenga wa Yehova anakanganuka pamaso pake. Pamenepo Gideoni anaona kuti ndiye mthenga wa Yehova, nati Gideoni, Tsoka ine, Yehova Mulungu! Popeza ndaona mthenga wa Yehova maso ndi maso. Ndipo Yehova anati kwa iye, Mtendere ukhale ndi iwe, usaope, sudzafa. Pamenepo Gideoni anammangira Yehova guwa la nsembe pomwepo; nalitcha Yehova-ndiye-mtendere; likali m'Ofura wa Aabiyezere ndi pano pomwe. Ndipo kunali, usiku womwe uja Yehova ananena naye, Tenga ng'ombe ya atate wako, ndiyo ng'ombe yachiwiri ya zaka zisanu ndi ziwiri, nugamule guwa la nsembe la Baala ndilo la atate wako, nulikhe chifanizo chili pomwepo; numangire Yehova Mulungu wako guwa la nsembe pamwamba pa lingali, monga kuyenera; nutenge ng'ombe yachiwiriyo, nufukize nsembe yopsereza; nkhuni zake uyese chifanizo walikhacho. Pamenepo Gideoni anatenga amuna khumi mwa anyamata ake, nachita monga Yehova adanena naye; ndipo kunali, popeza anaopa akunyumba ya atate wake, ndi amuna akumudziwo, sanachichite msana, koma usiku. Ndipo pakuuka mamawa amuna akumudziwo, taonani, guwa la nsembe la Baala litagamuka, ndi chifanizo chinali pomwepo chitalikhidwa ndi ng'ombe yachiwiri yoperekedwa pa guwa la nsembe adalimanga. Nanenana wina ndi mnzake, Wachita ichi ndani? Ndipo atafunafuna nafunsafunsa, anati, Gideoni, mwana wa Yowasi wachita ichi. Pamenepo amuna akumudziwo anati kwa Yowasi, Umtulutse mwana wako kuti afe; pakuti anagamula guwa la nsembe la Baala, pakutinso analikha chifanizo chinali pomwepo. Koma Yowasi anati kwa onse akumuimirira, Kodi inu mumnenera Baala mlandu? Kapena kodi mudzampulumutsa iye? Iye amene amnenera mlandu aphedwe kukali m'mawa; akakhala mulungu adzinenere yekha mlandu, popeza wina wamgamulira guwa lake la nsembe. Chifukwa chake anamutcha tsiku lija Yerubaala, ndi kuti, Amnenere mlandu Baala popeza anamgamulira guwa lake la nsembe. Pamenepo Amidiyani onse ndi Aamaleke ndi ana a kum'mawa anasonkhana pamodzi naoloka, namanga misasa m'chigwa cha Yezireele. Koma mzimu wa Yehova unavala Gideoni; naomba lipenga iye, ndi a banja la Abiyezere analalikidwa kumtsata iye. Ndipo anatuma mithenga kwa Manase konse; ndi iwonso analalikidwa kumtsata iye; natuma mithenga kwa Asere, ndi kwa Zebuloni, ndi kwa Nafutali; iwo nadzakomana nao. Ndipo Gideoni anati kwa Mulungu, Mukadzapulumutsa Israele ndi dzanja langa monga mwanena, taonani, ndidzaika chikopa cha ubweya popunthira tirigu; pakakhala mame pachikopa pokha, ndi panthaka ponse pouma, pamenepo ndidzadziwa kuti mudzapulumutsa Israele ndi dzanja langa monga mwanena. Ndipo kunatero; pakuti anauka mamawa, nafinya chikopacho, nakamula mame a pachikopa, madzi ake odzala mbale. Ndipo Gideoni ananena ndi Mulungu, Mkwiyo wanu usandiyakire, ndinene kamodzi kokha: ndikuyeseni kamodzi kokha ndi chikopa; paume pachikopa pokha, ndi panthaka ponse pakhale mame. Ndipo Mulungu anatero usiku uja; pakuti panauma pachikopa pokha, ndi panthaka ponse panali mame. Pamenepo Yerubaala, ndiye Gideoni, ndi anthu onse okhala naye anauka mamawa, namanga misasa pa chitsime cha Harodi, ndi misasa ya Midiyani inali kumpoto kwao, pa phiri la More m'chigwa. Ndipo Yehova anati kwa Gideoni. Anthu ali ndi iwe andichulukira kuti ndipereke Midiyani m'dzanja lao; angadzitame Israele pa Ine, ndi kuti, Dzanja la ine mwini landipulumutsa. Ndipo tsopano, kalalike m'makutu a anthu, ndi kuti, Aliyense wochita mantha, nanjenjemera, abwerere nachoke pa phiri la Giliyadi. Ndipo anabwererako anthu zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, natsalako zikwi khumi. Ndipo Yehova ananena ndi Gideoni, Anthu akali ochuluka; tsikira nao kumadzi, ndipo ndidzakuyesera iwo komweko; ndipo kudzali kuti iye amene ndimnena kwa iwe, Uyo azimuka nawe, yemweyo azimuka nawe; koma aliyense ndimnena kwa iwe, Uyo asamuke nawe, yemweyo asamuke. Ndipo anatsikira nao anthu kumadzi; ndipo Yehova anati kwa Gideoni, Aliyense akapiza madzi pa lilime lake, monga akhatira galu, ameneyo amuike pa yekha; momwemo aliyense agwada pakumwa. Ndi kuwerenga kwa iwo akukhatira, ndi kuika dzanja lao kukamwa kwao, ndiko mazana atatu; koma ena onse anagwada pakumwa madzi. Ndipo Yehova anati kwa Gideoni, Ndi anthu mazana atatu akukhatira ndidzakupulumutsani, ndi kupereka Amidiyani m'dzanja lako; koma amuke anthu awa onse, yense kumalo kwake. Pamenepo anthu anatenga kamba m'dzanja lao, ndi malipenga ao; ndipo anauza amuna onse a Israele amuke, yense kuhema kwake; koma anaimika amuna mazana atatuwo; ndipo misasa ya Midiyani inali kunsi kwake m'chigwa. Ndipo kunali usiku womwewo, kuti Yehova ananena naye, Tauka, tatsikira kumisasa; pakuti ndaipereka m'dzanja lako. Koma ngati uopa kutsika, utsike naye Pura mnyamata wako kumisasa; nudzamva zonena iwo; utatero manja ako adzalimbikitsidwa kutsikira kumisasa. Pamenepo anatsikira ndi Pura mnyamata wake ku chilekezero cha anthu azida a m'misasa. Ndipo Amidiyani ndi Aamaleke ndi ana onse a kum'mawa ali gonere m'chigwa, kuchuluka kwao ngati dzombe; ndi ngamira zao zosawerengeka, kuchuluka kwao ngati mchenga wa m'mphepete mwa nyanja. Ndipo pakufikako Gideoni, taonani, panali munthu analikufotokozera mnzake loto, nati, Taona, kulota ndinalota, ndipo tapenya, mtanda wa mkate wabarele unakunkhulirakunkhulira m'misasa ya Midiyani, nufika kuhema, numgunda nagwa, numpidigula kuti hema anakhala chigwere. Ndipo mnzake anayankha nati, Ichi si china konse koma lupanga la Gideoni mwana wa Yowasi, munthu wa Israele; Mulungu wapereka Midiyani ndi a m'misasa onse m'dzanja lake. Ndipo kunali, pakumva Gideoni kufotokozera kwa lotolo ndi tanthauzo lake, anadziwerama; nabwera ku misasa ya Israele nati, Taukani, pakuti Yehova wapereka a m'misasa a Midiyani m'dzanja lanu. Ndipo anagawa amuna mazana atatu akhale magulu atatu, napatsa malipenga m'manja a iwo onse, ndi mbiya zopanda kanthu, ndi miuni m'kati mwa mbiyazo. Ndipo ananena nao, Mundipenyerere ine, ndi kuchita momwemo; ndipo taonani, pakufika ine pa chilekezero cha misasa, kudzali, monga ndichita ine, momwemo muzichita inu. Pamene ndiomba lipenga, ine ndi onse okhala nane, inunso muziomba lipenga pozungulira ponse pa misasa, ndi kunena kuti, Yehova ndi Gideoni. Motero Gideoni ndi amuna zana anali naye anafikira ku chilekezero cha misasa poyambira ulonda wa pakati, atasintha alonda tsopano apa; ndipo anaomba malipenga, naphwanya mbiya zokhala m'manja mwao. Ndi magulu atatuwo anaomba malipenga, naswa mbiyazo, nagwira miuni ndi dzanja lao lamanzere, ndi malipenga m'dzanja lao lamanja kuwaomba; ndipo anafuula, Lupanga la Yehova ndi la Gideoni. Ndipo anaima yense m'mbuto mwake pozungulira misasa; pamenepo anathamanga a m'misasa onse, nafuula, nathawa. Ndipo mazana atatuwa anaomba malipenga, ndipo Yehova anakanthanitsa yense mnzake ndi lupanga m'misasa monse; ndi a m'misasa anathawa mpaka ku Betesita ku Zerera, mpaka ku malire a Abele-Mehola pa Tabati. Pamenepo anthu a Israele analalikidwa kuchokera ku Nafutali, ndi ku Asere, ndi ku Manase yense, nalondola Amidiyani. Gideoni anatumanso mithenga ku mapiri onse a Efuremu ndi kuti, Tsikani, kukomana ndi Amidiyani ndi kutsekereza madooko asanafike iwowa, mpaka ku Betebara ndi Yordani. Potero amuna onse a Efuremu anasonkhana pamodzi natsekereza madooko mpaka ku Betebara, ndi Yordani. Ndipo anagwira akalonga awiri a Midiyani, Orebu ndi Zeebu; namupha Orebu ku thanthwe la Orebu; ndi Zeebu anamupha ku choponderamo mphesa cha Zeebu, nalondola Amidiyani; ndipo anadza nayo mitu ya Orebu ndi Zeebu kwa Gideoni tsidya lija la Yordani. Ndipo amuna a Efuremu anati kwa iye, Ichi watichitira nchiyani, osatiitana popita iwe kulimbana ndi Amidiyani? Natsutsana naye kolimba. Koma ananena nao, Ndachitanji tsopano monga inu? Kodi kukunkha mphesa kwa Efuremu sikuposa kutchera mphesa kwa Abiyezere? Mulungu anapereka m'dzanja lanu akalonga a Midiyani, Orebu ndi Zeebu, ndipo ndinakhoza kuchitanji monga inu? Pamenepo mkwiyo wao unamlezera, atanena mau awa. Ndipo Gideoni anafika ku Yordani, naoloka, iye ndi amuna mazana atatu anali naye, ali otopa koma ali chilondolere. Ndipo ananena kwa amuna a ku Sukoti, Mupatsetu anthu awa akunditsata mitanda yamkate; pakuti atopa, ndipo ndilikulondola Zeba ndi Zalimuna mafumu a Midiyani. Koma akalonga a ku Sukoti anati, Kodi manja a Zeba ndi Zalimuna ali m'dzanja lako tsopano apa, kuti ife tiwaninkhe ankhondo ako mkate? Ndipo Gideoni anati, Chifukwa chake, Yehova akapereka Zeba ndi Zalimuna m'dzanja langa, ndidzapuntha nyama yanu ndi minga ya m'chipululu ndi mitungwi. Ndipo anachokapo kukwera ku Penuwele, nanena nao momwemo; ndipo amuna a ku Penuwele anamyankha monga adamyankha amuna a ku Sukoti. Ndipo ananenanso kwa amuna a ku Penuwele ndi kuti, Ndikabwerera ndi mtendere ndidzagumula nsanja iyi. Zeba ndi Zalimuna ndipo anali m'Karikori, ndi a m'misasa ao pamodzi nao, amuna monga zikwi khumi ndi zisanu; ndiwo otsala onse a khamu lonse la ana a kum'mawa; popeza atagwa amuna zikwi zana limodzi ndi makumi awiri akusolola lupanga. Ndipo Gideoni anakwerera njira ya iwo okhala m'mahema kum'mawa kwa Noba, ndi Yogobeha, nakantha khamulo popeza khamulo linakhala lokhazikika mtima. Ndipo Zeba ndi Zalimuna anathawa; koma anawatsata, nagwira mafumu awiri a Midiyani Zeba ndi Zalimuna, nanjenjemeretsa khamu lonse. Pamenepo Gideoni mwana wa Yowasi anabwerera kunkhondo pokwerera pa Heresi. Ndipo anagwira mnyamata wa anthu a ku Sukoti, nafunsira; ndipo anamsimbira akalonga a ku Sukoti, ndi akulu ake amuna makumi asanu ndi awiri kudza asanu ndi awiri. Ndipo anafika kwa amuna a ku Sukoti, nati, Tapenyani Zeba ndi Zalimuna amene munanditonza nao ndi kuti, Kodi manja a Zeba ndi Zalimuna akhala m'dzanja lako, kuti tiwaninkhe mkate amuna ako akulema? Ndipo anagwira akulu a m'mudzi ndi minga ya kuchipululu ndi mitungwi, nawalanga nazo amuna a ku Sukoti. Ndipo anagamula nsanja ya Penuwele, napha amuna akumudzi. Pamenepo anati kwa Zeba ndi Zalimuna, Amunawo munawapha ku Tabori anali otani? Iwo nayankha, Monga iwe momwemo iwowa; yense wakunga mwana wa mfumu. Ndipo anati, Ndiwo abale anga, ana a mai wanga. Pali Yehova mukadawasunga amoyo, sindikadakuphani. Nati kwa Yetere mwana wake woyamba, Tauka, nuwaphe. Koma mnyamatayo sanasolole lupanga lake; pakuti anaopa, pokhala anali mnyamata. Pamenepo Zeba ndi Zalimuna anati, Tauka iwe mwini nutigwere; pakuti monga munthu momwemo mphamvu yake. Ndipo Gideoni anauka nawapha Zeba ndi Zalimuna, nalanda mphande zinali kukhosi kwa ngamira zao. Pamenepo anthu a Israele anati kwa Gideoni, Mutilamulire ndi inu, ndi mwana wanu, ndi mdzukulu wanu, pakuti mwatipulumutsa m'dzanja la Amidiyani. Koma Gideoni ananena nao. Sindidzalamulira inu, ngakhale mwana wanga sadzalamulira inu; Yehova adzalamulira inu. Gideoni anatinso kwa iwo, Mundilole ndipemphe kanthu kamodzi kwa inu, mundipatse aliyense maperere mwa zofunkha zanu; pakuti anali nao maperere agolide, pokhala anali Aismaele. Ndipo anayankha, Kupereka tiwapereka; nayalapo chovala, naponyamo yense maperere a mwa zofunkha zao. Ndipo kulemera kwake kwa maperere agolide adawapempha ndiko masekeli chikwi chimodzi ndi mazana asanu ndi awiri; osawerenga mphande, ndi zitunga ndi zovala zachibakuwa za pa mafumu a ku Midiyani, osawerenganso maunyolo okhala pa makosi a ngamira zao. Ndipo Gideoni anawapanga fano, naliika m'mudzi mwake, ndiwo Ofura; ndi Israele yense analitsata kuligwadira pomwepo; ndipo linakhala kwa Gideoni ndi nyumba yake ngati msampha. Motero anagonjetsa Amidiyani pamaso pa ana a Israele, osaweramutsanso mitu yao iwowa. Ndipo dziko lidapumula zaka makumi anai m'masiku a Gideoni. Ndipo Yerubaala, mwana wa Yowasi anamuka, nakhala m'nyumba ya iye yekha. Nakhala nao ana amuna makumi asanu ndi awiri Gideoni, anawabala ndi iye; popeza anali nao akazi ambiri. Ndipo mkazi wake wamng'ono wokhala m'Sekemu, iyenso anambalira mwana wamwamuna; namutcha dzina lake Abimeleki. Ndipo Gideoni mwana wa Yowasi anafa atakalamba bwino, naikidwa m'manda a Yowasi atate wake, m'Ofura wa Aabiyezere. Ndipo kunali, atafa Gideoni, ana a Israele anabwereranso nagwadira Abaala, nayesa Baala-Beriti mulungu wao. Ndi ana a Israele sanakumbukire Yehova Mulungu wao, amene anawapulumutsa m'dzanja la adani ao onse pozungulira ponse; osachitira chifundo nyumba ya Yerubaala, ndiye Gideoni, monga mwa zokoma zonse iye anachitira Israele. Koma Abimeleki mwana wa Yerubaala anamuka ku Sekemu kwa abale a amai wake, nanena nao, ndi kwa banja lonse la nyumba ya atate wa amai wake, ndi kuti, Nenanitu m'makutu mwa eni ake onse a ku Sekemu, Chokomera inu nchiti, akulamulireni ana amuna onse a Yerubaala ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, kapena akulamulireni mwamuna mmodzi? Mukumbukirenso kuti ine ndine wa fuko lanu ndi nyama yanu. Pamenepo abale a amake anamnenera mau awa onse m'makutu a eni ake onse a Sekemu; ndi mitima yao inalunjika kutsata Abimeleki; pakuti anati, Ndiye mbale wathu. Ndipo anampatsa ndalama makumi asanu ndi awiri za m'nyumba ya Baala-Beriti; ndipo Abimeleki analembera nazo anthu opanda pake ndi opepuka amene anamtsata. Ndipo anamuka kunyumba ya atate wake ku Ofura, nawapha abale ake ana a Yerubaala, ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, pa thanthwe limodzi; koma Yotamu mwana wamng'ono wa Yerubaala anatsalako; pakuti anabisala. Pamenepo anasonkhana eni ake onse a ku Sekemu, ndi nyumba yonse ya Milo, namuka namlonga Abimeleki ufumu pa thundu wa choimiritsa chili m'Sekemu. Ndipo atamuuza Yotamu, anamuka iye naimirira pamutu pa phiri la Gerizimu, nakweza mau ake, nafuula, nanena nao, Mundimvere ine, eni ake a ku Sekemu inu, kuti Mulungu amvere inu. Kumuka inamuka mitengo kudzidzozera mfumu; niti kwa mtengo wa azitona, Ukhale iwe mfumu yathu. Koma mtengo wa azitona unati kwa iwo, Ngati ndidzasiya kunona kwanga kumene alemekeza nako Mulungu ndi anthu kukalenga pa mitengo? Pamenepo mitengo inati kwa mkuyu. Tiye iwe, ukhale mfumu yathu. Koma mkuyu unanena nao, Ngati ndidzasiya kuzuna kwanga, ndi zipatso zanga zokoma kukalenga pa mitengo? Pamenepo mitengo inati kwa mpesa, Tiye iwe, ukhale mfumu yathu. Koma mpesa unanena nao, Ngati ndidzasiya vinyo wanga wakusekeretsa Mulungu ndi anthu, kukalenga pa mitengo? Pamenepo mitengo yonse inati kwa nkandankhuku, Tiye iwe, ukhale mfumu yathu. Ndipo nkandankhuku unati kwa mitengo, Mukandidzoza mfumu yanu moonadi, tiyeni, thawirani ku mthunzi wanga; mukapanda kutero utuluke moto m'nkandankhuku ndi kunyeketsa mikungudza ya Lebanoni. Ndipo tsopano, ngati mwachita moona ndi mwangwiro pakulonga Abimeleki ufumu, ngatinso mwamchitira chokoma Yerubaala ndi nyumba yake, ndi kumchitira monga anayenera manja ake; pakuti atate wanga anakugwirirani nkhondo, nataya moyo wake, nakupulumutsani m'dzanja la Amidiyani; koma mwaukira nyumba ya atate wanga lero lino, ndi kuwapha ana ake, ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, pa thanthwe limodzi; ndipo mwalonga Abimeleki mwana wa mdzakazi wake, akhale mfumu ya pa eni ake a ku Sekemu, chifukwa ali mbale wanu; ngati tsono mwachitira Yerubaala ndi nyumba yake zoona ndi zangwiro lero lino, kondwerani naye Abimeleki, nayenso akondwere nanu; koma ngati simunatero, utuluke moto kwa Abimeleki, nunyeketse eni ake a ku Sekemu ndi nyumba ya Milo; nutuluke moto kwa eni ake a ku Sekemu, ndi kunyumba yake ya Milo, nunyeketse Abimeleki. Pamenepo Yotamu anafulumira, nathawa, namuka ku Beere, nakhala komweko, chifukwa cha Abimeleki mbale wake. Abimeleki atakhala kalonga wa Israele zaka zitatu, Mulungu anatumiza mzimu woipa pakati pa Abimeleki ndi eni ake a ku Sekemu; ndi eni ake a ku Sekemu anamchitira Abimeleki mosakhulupirika; kuti chiwawa adachitira ana amuna makumi asanu ndi awiri a Yerubaala chimdzere, ndi kuti mwazi wao uikidwe pa mbale wao Abimeleki anawaphayo, ndi pa eni ake a ku Sekemu, amene analimbikitsa manja ake, awaphe abale ake. Ndipo eni ake a ku Sekemu anaika omlalira pamwamba pa mapiri; amene anawawanya onse akudzera njirayi; ndipo anamuuza Abimeleki. Ndipo Gaala, mwana wa Ebedi anadza ndi abale ake, napita ku Sekemu; ndi eni ake a ku Sekemu anamkhulupirira. Ndipo anatuluka kunka kuminda, natchera mphesa m'mindamo, naponda mphesa, napereka nsembe yolemekeza, nalowa m'nyumba ya mulungu wao, nadya, namwa, natemberera Abimeleki. Pamenepo Gaala, mwana wa Ebedi anati, Abimeleki ndani, ndi Sekemu ndani, kuti timtumikire? Sindiye mwana wa Yerubaala kodi? Ndi Zebuli kazembe wake? Mutumikire amuna a Hamori atate wa Sekemu; koma ameneyo timtumikire chifukwa ninji? Mwenzi anthu awa akadakhala m'dzanja langa; ndikadamchotsadi Abimeleki. Ndipo anati kwa Abimeleki, Chulukitsa khamu lako, nutuluke. Pamene Zebuli woyang'anira mudzi anamva mau a Gaala mwana wa Ebedi, anapsa mtima. Natuma mithenga kwa Abimeleki ku Aruma monyenga nati, Taonani Gaala mwana wa Ebedi ndi abale ake afika ku Sekemu; ndipo taonani, akupandukitsirani mudzi. Ndipo tsopano, taukani usiku, inu ndi anthu okhala nanu ndi kulalira kuthengo; ndipo kukhale kuti m'mawa, pakutuluka dzuwa, muuke mamawa mugwere mudziwo; ndipo taonani, akakutulukirani iye ndi anthu ali naye, uzimchitira monga lidziwa dzanja lako. Pamenepo Abimeleki anauka ndi anthu onse anali naye, usiku; nalalira a ku Sekemu, magulu anai. Ndipo Gaala mwana wa Ebedi anatuluka, naima polowera pa chipata cha mudzi; naika Abimeleki ndi anthu anali naye m'molalira. Ndipo pamene Gaala anapenya anthuwo anati kwa Zebuli, Taona, alikutsika anthu kuchokera pamwamba pa mapiri. Koma Zebuli ananena naye, Uona mthunzi wa mapiri ndi kuyesa anthu. Koma Gaala ananenanso, nati, Tapenya alikutsika anthu pakati pa dziko, ndi gulu limodzi lidzera njira ya ku thundu wa alauli. Pamenepo Zebuli anati kwa iye, Pakamwa pako mpoti tsopano, muja udanena, Ndani Abimeleki kuti timtumikire? Awa si anthuwo unawapeputsa? Utuluke tsopano, nulimbane nao. Ndipo Gaala anatuluka pamaso pao pa eni ake a ku Sekemu, nalimbana ndi Abimeleki. Koma Abimeleki anampirikitsa, nathawa iye pamaso pake; nagwa olasidwa ambiri mpaka polowera pa chipata. Ndipo Abimeleki anakhala ku Aruma; ndi Zebuli anaingitsa Gaala ndi abale ake kuti asakhale m'Sekemu. Ndipo kunali m'mawa mwake, kuti anthu anatuluka kunka kuminda; ndipo anauza Abimeleki. Pamenepo anatenga anthu, nawagawa magulu atatu, nalalira m'minda; napenya, ndipo taonani, anthu alimkutuluka m'mudzi; nawaukira iye nawakantha. Ndi Abimeleki ndi magulu okhala naye anathamanga naima polowera pa chipata cha mudzi; ndi magulu awiriwo anagwera onse okhala m'munda, nawakantha. Ndipo Abimeleki analimbana ndi mudzi tsiku lija lonse; nalanda mudzi nawapha anthu anali m'mwemo; napasula mudzi; nawazapo mchere. Ndipo pamene eni ake onse a nsanja ya ku Sekemu anachimva, analowa m'ngaka ya nyumba ya Eliberiti. Ndipo anauza Abimeleki kuti amuna onse a nsanja ya ku Sekemu asonkhane. Pamenepo Abimeleki anakwera kunka kuphiri la Zalimoni, iye ndi anthu onse anali naye; natenga nkhwangwa m'dzanja lake Abimeleki, nadula nthambi kumitengo, nainyamula ndi kuiika paphewa pake, nati kwa anthu okhala naye, Ichi munachiona ndachita, fulumirani, muchite momwemo. Ndi anthu onse anadulanso yense nthambi yake, natsata Abimeleki, naziika pangaka, natentha nazo ngakayo ndi moto; motero anthu onse a nsanja ya ku Sekemu anafanso, amuna ndi akazi ngati chikwi chimodzi. Pamenepo Abimeleki anamuka ku Tebezi, naumangira Tebezi misasa, naulanda. Koma m'mudzimo munali nsanja yolimba nathawira kumeneko amuna ndi akazi onse, ndi eni ake onse a mudziwo, nadzitsekereza m'mwemo, nakwera patsindwi pa nsanja. Ndipo Abimeleki anafika kunsanja, nalimbana nayo nkhondo, nayandikira kukhomo kwa nsanja, aitenthe ndi moto. Ndipo mkazi wina anaponya mwana wa mphero pamutu pa Abimeleki, naphwanya bade lake. Pamenepo anaitana msanga mnyamata wake wosenza zida zake, nanena naye, Solola lupanga lako nundiphe, angamanenere anthu, ndi kuti, Anamupha ndi mkazi. Nampyoza mnyamata wake, nafa iye. Pamene amuna a Israele anaona kuti adafa Abimeleki anamuka yense kumalo kwake. Momwemo Mulungu anambwezera Abimeleki choipacho anachitira atate wake ndi kuwapha abale ake makumi asanu ndi awiri. Ndipo Mulungu anawabwezera choipa chonse cha amuna a ku Sekemu pamitu pao, ndipo linawagwera temberero la Yotamu mwana wa Yerubaala. Atafa Abimeleki, anauka kupulumutsa Israele Tola mwana wa Puwa, mwana wa Dodo munthu wa Isakara; nakhala iye m'Samiri ku mapiri a Efuremu. Ndipo anaweruza Israele zaka makumi awiri ndi zitatu, nafa, naikidwa m'Samiri. Atafa iye, anauka Yairi Mgiliyadi, naweruza Israele zaka makumi awiri mphambu ziwiri. Ndipo anali nao ana amuna makumi atatu okwera pa ana a abulu makumi atatu, iwo ndipo anali nayo midzi makumi atatu, otchedwa midzi ya Yairi, mpaka lero lino, ndiyo m'dziko la Giliyadi. Nafa Yairi, naikidwa m'Kamoni. Ndipo ana a Israele anaonjeza kuchita choipa pamaso pa Yehova, natumikira Abaala, ndi Aasitaroti, ndi milungu ya Aramu, ndi milungu ya Sidoni, ndi milungu ya Mowabu, ndi milungu ya ana a Amoni, ndi milungu ya Afilisti; ndipo anamleka Yehova osamtumikira. Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele, nawagulitsa m'dzanja la Afilisti, ndi m'dzanja la ana a Amoni. Ndipo anaphwanya napsinja ana a Israele chaka chija, natero ndi ana onse a Israele okhala tsidya lija la Yordani m'dziko la Aamori, ndilo Giliyadi, zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu. Ndipo ana a Amoni anaoloka Yordani kuthiranso nkhondo Yuda ndi Benjamini, ndi nyumba ya Efuremu; napsinjika kwambiri Israele. Ndipo ana a Israele anafuula kwa Yehova ndi kuti, Takuchimwirani, popeza tasiya Mulungu wathu ndi kutumikira Abaala. Ndipo Yehova anati kwa ana a Israele, Kodi sindinakupulumutsani kwa Aejipito ndi kwa Aamori, ndi kwa ana a Amoni, ndi kwa Afilisti? Asidoni omwe, ndi Aamaleke, ndi Amaoni anakupsinjani. Pamenepo munafuula kwa Ine, ndipo ndinakupulumutsani m'dzanja lao. Koma mwandisiya Ine ndi kutumikira milungu ina, chifukwa chake sindikupulumutsaninso. Mukani ndi kufuulira kwa milungu munaisankha, ikupulumutseni nyengo ya kusauka kwanu. Koma ana a Israele anati kwa Yehova, Tachimwa, mutichitire monga mwa zonse zikomera pamaso panu; komatu mutipulumutse lero lino, tikupemphani. Pamenepo anachotsa milungu yachilendo pakati pao, natumikira Yehova; ndipo mtima wake unagwidwa chisoni chifukwa cha mavuto a Israele. Ndipo ana a Amoni analalikiridwa, namanga misasa m'Giliyadi. Ndi ana a Israele anasonkhana namanga misasa ku Mizipa. Ndipo anthu, akalonga a Giliyadi, ananenana wina ndi mnzake, Ndaniyo adzayamba kulimbana ndi ana a Amoni? Iye adzakhala mkulu wa onse okhala m'Giliyadi. Yefita Mgiliyadi ndipo anali ngwazi yamphamvu, ndiye mwana wa mkazi wadama; koma Giliyadi adabala Yefita. Ndipo mkazi wa Giliyadi anambalira ana amuna; koma atakula ana amuna a mkaziyo anampirikitsa Yefita, nanena naye, Sudzalandira cholowa m'nyumba ya atate wako; pakuti ndiwe mwana wa mkazi wina. Pamenepo Yefita anathawa abale ake, nakhala m'dziko la Tobu; ndipo anyamata opanda pake anasonkhana kwa Yefita, natuluka naye pamodzi. Ndipo kunali, atapita masiku, ana a Amoni anachita nkhondo ndi Israele, ndipo kunatero, pamene ana a Amoni anathira nkhondo pa Israele, akulu a Giliyadi anamuka kutenga Yefita m'dziko la Tobu; nati kwa Yefita, Tiye ukhale kazembe wathu kuti tilimbane ndi ana a Amoni. Ndipo Yefita anati kwa akulu a Giliyadi, Simunandida kodi, ndi kundichotsa m'nyumba ya atate wanga? Ndipo mundidzeranji tsopano pokhala muli m'kusauka? Ndipo akulu a Giliyadi ananena ndi Yefita, Chifukwa chake chakuti takubwerera tsopano ndicho kuti umuke nafe ndi kuchita nkhondo ndi ana a Amoni, nudzakhala mkulu wathu wa pa onse okhala m'Giliyadi. Ndipo Yefita anati kwa akulu a Giliyadi, Mukandifikitsanso kwathu kuchita nkhondo ndi ana a Amoni, nakawapereka Yehova pamaso panga, ndidzakhala mkulu wanu kodi? Ndipo akulu a Giliyadi anati kwa Yefita, Yehova ndiye wakumvera pakati pa ife, tikapanda kuchita monga momwe wanena. Pamenepo Yefita anamuka ndi akulu a Giliyadi, ndipo anthu anamuika mkulu wao ndi mtsogoleri wao; ndipo Yefita ananena mau ake onse pamaso pa Yehova ku Mizipa. Ndipo Yefita anatuma mithenga kwa mfumu ya ana a Amoni, ndi kuti, Ndi chiyani ndi inu ndi kuti mwandidzera kuthira nkhondo dziko langa? Ndipo mfumu ya ana a Amoni inati kwa mithenga ya Yefita, Chifukwa Israele analanda dziko langa pakukwera iye kuchokera ku Ejipito, kuyambira Arinoni mpaka Yaboki, ndi mpaka Yordani; ndipo tsopano undibwezere maikowa mwamtendere. Ndipo Yefita anatumanso mithenga kwa mfumu ya ana a Amoni; nanena naye, Atero Yefita, Israele sanalande dziko la Mowabu kapena dziko la ana a Amoni; pakuti pakukwera iwo kuchokera ku Ejipito Israele anayenda m'chipululu mpaka Nyanja Yofiira, nafika ku Kadesi; pamenepo Israele anatuma mithenga kwa mfumu ya Edomu, ndi kuti, Ndikupemphani ndipitire pakati pa dziko lanu; koma mfumu ya Edomu siinamvera. Natumanso kwa mfumu ya Mowabu; nayenso osalola; ndipo Israele anakhala m'Kadesi. Pamenepo anayenda m'chipululu, naphazira dziko la Edomu, ndi dziko la Mowabu, nadzera kum'mawa kwa dziko la Mowabu, namanga misasa tsidya lija la Arinoni; osalowa malire a Mowabu, pakuti Arinoni ndi malire a Mowabu. Ndipo Israele anatuma mithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, mfumu ya ku Hesiboni; nanena naye Israele, Tikupemphani tipitire pakati pa dziko lanu, kunka kwathu. Koma Sihoni sanakhulupirire Israele kuti apitire pakati pa malire ake; koma Sihoni anamemeza anthu ake onse, namanga misasa ku Yahazi, nathira nkhondo Israele. Ndipo Yehova Mulungu wa Israele anapereka Sihoni ndi anthu ake onse m'dzanja la Israele, ndipo anawakantha, ndi Israele, analandira cholowa chake, dziko lonse la Aamori, nzika za m'dziko lija. Ndipo analandira akhale cholowa chao, malire onse a Aamori, kuyambira Arinoni mpaka Yaboki, ndi kuyambira chipululu mpaka Yordani. Motero Yehova Mulungu wa Israele anaingitsa Aamori, pamaso pa anthu ake Israele, ndipo kodi liyenera kukhala cholowa chanu? Chimene akulandiritsani Kemosi mulungu wanu, simuchilandira cholowa chanu kodi? Momwemo aliyense Yehova Mulungu wathu waingitsa pamaso pathu, zakezo tilandira cholowa chathu. Ndipo tsopano kodi inu ndinu wabwino woposa Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu; anatengana konse ndi Israele iyeyu kodi, kapena kuchita nao nkhondo konse kodi? Pokhala Israele m'Hesiboni ndi midzi yake, ndi m'Aroere ndi midzi yake ndi m'midzi yonse yokhala m'mphepete mwa Arinoni zaka mazana atatu; munalekeranji kulandanso nthawi ija? Potero sindinakuchimwirani ine, koma mundichitira choipa ndinu kundithira nkhondo; Yehova Woweruzayo, aweruze lero lino pakati pa ana a Israele ndi ana a Amoni. Koma mfumu ya ana a Amoni sanamvere mau a Yefita anamtumizirawo. Pamenepo mzimu wa Yehova unamdzera Yefita, napitira iye ku Giliyadi, ndi Manase, napitira ku Mizipa wa Giliyadi, ndi kuchokera ku Mizipa wa Giliyadi anapitira kwa ana a Amoni. Ndipo Yefita anawindira Yehova chowinda, nati, Mukaperekatu ana a Amoni m'dzanja langa, ndipo kudzali kuti chilichonse chakutuluka pakhomo pa nyumba yanga kudzakomana nane pakubweranso ine ndi mtendere kuchokera kwa ana a Amoni, chidzakhala cha Yehova, ndipo ndidzachipereka nsembe yopsereza. Potero Yefita anapita kwa ana a Amoni kuwathira nkhondo; ndipo Yehova anawapereka m'dzanja lake; nawakantha kuyambira ku Aroere mpaka ufika ku Miniti, ndiyo midzi makumi awiri, ndi ku Abele-Keranimu, makanthidwe akulu ndithu. Motero ana a Amoni anagonjetsedwa pamaso pa ana a Israele. Pofika Yefita ku Mizipa kunyumba yake, taonani, mwana wake wamkazi anatuluka kudzakomana naye ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe; ndipo iyeyu anali mwana wake mmodzi yekha, analibe mwana wina wamwamuna kapena wamkazi. Ndipo kunali, pakumuona anang'amba zovala zake, nati, Tsoka ine, mwana wanga, wandiweramitsa kwakukulu, ndiwe wa iwo akundisaukitsa ine; pakuti ndamtsegulira Yehova pakamwa panga ine, ndipo sinditha kubwerera. Ndipo anati kwa iye, Atate wanga, mwamtegulira Yehova pakamwa panu, mundichitire ine monga umo mudatulutsa mau pakamwa panu; popeza Yehova anakuchitirani inu chilango pa adani anu, pa ana a Amoni. Ndipo anati kwa atate wake, Andichitire ichi, andileke miyezi iwiri, kuti ndichoke ndi kutsikira kumapiri, ndi kulirira unamwali wanga, ine ndi anzanga. Nati iye, Muka. Namuuza amuke akakhale miyezi iwiri; namuka iye ndi anzake, nalirira unamwali wake pamapiri. Ndipo kunali pakutha miyezi iwiri, anabwerera kwa atate wake amene anamchitira monga mwa chowinda chake anachiwinda; ndipo sanamdziwe mwamuna. Motero unali mwambo m'Israele, kuti ana akazi a Israele akamuka chaka ndi chaka kumliririra mwana wa Yefita wa ku Giliyadi, masiku anai pa chaka. Pamenepo amuna a Efuremu analalikidwa, napita kumpoto; nati kwa Yefita, Wapitiriranji kuthira nkhondo ana a Amoni, osatiitana ife timuke nawe? Tidzakutenthera nyumba yako ndi moto pamtu pako. Ndipo Yefita anati kwa iwo, Ine ndi anthu anga tinatsutsana kwakukulu ndi ana a Amoni, koma pamene ndinakuitanani inu simunandipulumutsa m'dzanja lao. Ndipo pakuona ine kuti simundipulumutsa, ndinataya moyo wanga ndi kupita kwa ana a Amoni; ndipo Yehova anawapereka m'dzanja langa; mwakwereranji tsono lero lino kundichitira nkhondo? Pamenepo Yefita anamemeza amuna onse a m'Giliyadi nalimbana naye Efuremu; ndipo amuna a Giliyadi anakantha Efuremu, chifukwa adati, Inu Agiliyadi ndinu akuthawa Efuremu, pakati pa Efuremu ndi pakati pa Manase. Ndipo Agiliyadi anatsekereza madooko a Yordani a Efuremu; ndipo kunatero kuti, akati othawa a Efuremu, Ndioloke, amuna a Giliyadi anati kwa Iye, Ndiwe Mwefuremu kodi? Akati, Iai; pamenepo anati kwa iye, Unene tsono Shiboleti; ndipo akati, Siboleti, osakhoza kutchula bwino, amgwira namupha padooko pomwe pa Yordani; ndipo anagwa a Efuremu nthawi ija, zikwi makumi anai mphambu ziwiri. Ndipo Yefita anaweruza Israele zaka zisanu ndi chimodzi; nafa Yefita Mgiliyadi, naikidwa m'mudzi wina wa Giliyadi. Ndi pambuyo pake Ibizani wa ku Betelehemu anaweruza Israele. Ndipo anali nao ana amuna makumi atatu; ndi ana akazi makumi atatu anawakwatitsa kwina, natengera ana ake amuna ana akazi makumi atatu ochokera kwina. Ndipo anaweruza Israele zaka zisanu ndi ziwiri. Nafa Ibizani naikidwa ku Betelehemu. Ndi pambuyo pake Eloni Mzebuloni anaweruza Israele; naweruza Israele zaka khumi. Nafa Eloni Mzebuloni naikidwa m'Ayaloni m'dziko la Zebuloni. Ndi pambuyo pake Abidoni mwana wa Hilele wa ku Piratoni anaweruza Israele. Ndipo anali nao ana amuna makumi anai ndi zidzukulu zazimuna makumi atatu, akuyenda okwera pa ana a abulu makumi asanu ndi awiri; naweruza Israele zaka zisanu ndi zitatu. Nafa Abidoni mwana wa Hilele wa ku Piratoni, naikidwa m'Piratoni m'dziko la Efuremu ku mapiri a Amaleke. Ndipo ana a Israele anaonjeza kuchita choipa pamaso pa Yehova; nawapereka Yehova m'dzanja la Afilisti zaka makumi anai. Ndipo panali munthu wina wa Zora wa banja la Adani, dzina lake ndiye Manowa; ndi mkazi wake analibe mwana, sanabala. Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera mkaziyo nanena naye, Taona tsopano, ulibe mwana wosabala iwe; koma udzaima ndi kubala mwana wamwamuna. Chifukwa chake udzisamalire, usamwe vinyo kapena choledzeretsa, nusadye chinthu chilichonse chodetsa; pakuti taona, udzaima, nudzabala mwana wamwamuna; pamutu pake sipadzafika lumo; pakuti mwanayo adzakhalira kwa Mulungu Mnaziri chibadwire; nadzayamba iye kupulumutsa Israele m'dzanja la Afilisti. Pamenepo anadza mkaziyo, nanena ndi mwamuna wake ndi kuti, Wandidzera munthu wa Mulungu; maonekedwe ake ndiwo ngati maonekedwe a mthenga wa Mulungu oopsa ndithu; ndipo sindinamfunsa uko achokera kapena sanandiuzenso dzina lake; koma anati kwa ine, Taona, udzaima, ndi kubala mwana wamwamuna; ndipo tsopano usamwe vinyo kapena choledzeretsa, nusadye chilichonse chodetsa; pakuti mwanayo adzakhalira kwa Mulungu Mnaziri chibadwire mpaka tsiku la kufa kwake. Pamenepo Manowa anapembedza Yehova, nati, Yehova, ndikupemphani, atidzerenso munthu wa Mulungu mudamtumayo, natilangize icho tizichitira mwanayo akadzabadwa. Ndipo Mulungu anamvera mau a Manowa; ndi mthenga wa Mulungu anamdzeranso mkaziyo, pamene anali m'munda, mwamuna wake Manowa palibe. Ndipo mkaziyo anafulumira nathamanga, nauza mwamuna wake, nanena naye, Taona, wandionekera munthu anandidzerayo tsiku lija. Nanyamuka Manowa natsata mkazi wake, namdzera mwamuna uja, nanena naye, Kodi ndinu mwamuna uja munalankhula ndi mkaziyu? Ndipo anati, Ndine amene. Nati Manowa, Achitike tsopano mau anu; koma makhalidwe ake a mwanayo ndi machitidwe ake adzatani? Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa Manowa, Zonse ndinazinena ndi mkazi azisamalire. Chilichonse chichokera kumpesa asadyeko, asamwe vinyo kapena choledzeretsa, kapena kudya chilichonse chodetsa; zonse ndinamlamulira azisunge. Ndipo Manowa anati kwa mthenga wa Yehova, Tiloleni tikuchedwetseni kuti tikukonzereni mwanawambuzi. Koma mthenga wa Yehova anati kwa Manowa, Ungakhale undichedwetsa, sindidzadya mkate wako; ndipo ukakonza nsembe yopsereza, uziipereka kwa Yehova. Pakuti Manowa sanadziwe kuti ndiye mthenga wa Yehova. Ndipo Manowa anati kwa mthenga wa Yehova, Dzina lanu ndani, kuti, atachitika mau anu, tikuchitireni ulemu. Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Ufunsiranji dzina langa, popeza lili lodabwitsa? Pamenepo Manowa anatenga mwanawambuzi pamodzi ndi nsembe yaufa, nazipereka kwa Yehova pathanthwe; ndipo mthengayo anachita modabwitsa, ndi Manowa ndi mkazi wake ali chipenyere. Pakuti kunali, pakukwera lawi la moto pa guwa la nsembe kumwamba, mthenga wa Yehova anakwera m'lawi la pa guwalo; ndi Manowa ndi mkazi wake ali chipenyere; nagwa iwowa nkhope zao pansi. Ndipo mthenga wa Yehova sanaonekerenso kwa Manowa kapena kwa mkazi wake. Pamenepo anadziwa Manowa kuti ndiye mthenga wa Yehova. Nati Manowa kwa mkazi wake, Tidzafa ndithu pakuti taona Mulungu. Koma mkazi wake ananena naye, Yehova akadafuna kutipha, sakadalandira nsembe yopsereza ndi nsembe yaufa pa dzanja lathu, kapena kutionetsa izi zonse, kapena kutimvetsa zoterezi nthawi yino. Ndipo mkaziyo anabala mwana wamwamuna namutcha dzina lake Samisoni; nakula mwanayo, Yehova namdalitsa. Ndipo mzimu wa Yehova unayamba kumfulumiza mtima ku misasa ya Dani pakati pa Zora ndi Esitaoli. Ndipo Samisoni anatsikira ku Timna, naona mkazi wa ku Timna wa ana akazi a Afilisti. Nakwera iye, nauza atate wake ndi amai wake, nati, Ndapenya mkazi m'Timna wa ana akazi a Afilisti; ndipo tsono munditengere uyu akhale mkazi wanga. Koma atate wake ndi amai wake ananena naye, Kodi palibe mkazi mwa ana akazi a abale ako, kapena mwa anthu a mtundu wanga onse, kuti wamuka kutenga mkazi wa Afilisti osadulidwawo? Nati Samisoni kwa atate wake, Nditengereni iye, pakuti andikonda pamaso panga. Koma atate wake ndi amai wake sanadziwe kuti chidachokera kwa Yehova ichi; popeza analikufuna kutola chifukwa ndi Afilisti. Ndipo nthawi ija Afilisti analamulira Israele. Pamenepo anatsikira Samisoni, ndi atate wake ndi mai wake ku Timna, nadza ku minda yamphesa ya Timna; ndipo taona, mwana wa mkango wakomana naye namdzumira. Ndipo unamgwera iye kolimba mzimu wa Yehova, naung'amba monga akadang'amba mwanawambuzi, wopanda kanthu m'dzanja lake; koma sanauze atate wake kapena amai wake chimene adachichita. Ndipo anatsika nakamba ndi mkazi, namkonda Samisoni pamaso pake. Atapita masiku ndipo anabweranso kudzamtenga, napatuka iye kukaona mtembo wa mkango; ndipo taona, m'chitanda cha mkango munali njuchi zoundana, ndi uchi. Ndipo anaufula ndi dzanja lake, nayenda, namadya alimkuyenda, nadza kwa atate wake ndi amai wake, nawapatsa, nadya iwo; koma sanawauze kuti adaufula uchiwo m'chitanda cha mkango. Ndipo atate wake anatsikira kwa mkazi; ndi Samisoni anakonzerapo madyerero; pakuti amatero anyamata. Ndipo kunali, pamene anamuona, anabwera nao anzake makumi atatu akhale naye. Nanena nao Samisoni, Mundilole ndikuphereni mwambi; mukanditanthauziratu uwu m'masiku asanuwa a madyerero, ndi kumasulira uwu, ndidzakupatsani malaya a nsalu yabafuta makumi atatu ndi zovala zosinthanitsa makumi atatu; koma ngati simukhoza kunditanthauzira uwu mudzandipatsa ndinu malaya a nsalu yabafuta makumi atatu ndi zovala zosinthanitsa makumi atatu. Pamenepo ananena naye, Mwambi wako tiumve. Ndipo ananena nao, Chakudya chinatuluka m'mwini kudya, ndi chozuna chinatuluka m'mwini mphamvu. Ndipo masiku atatu sanakhoze kutanthauzira mwambiwo. Koma kunali, tsiku lachisanu ndi chiwiri anati kwa mkazi wa Samisoni, Kopa mwamuna wako, atitanthauzire mwambiwo; tingatenthe iwe ndi nyumba ya atate wako ndi moto. Kodi mwatiitana kulanda zathu; si momwemo? Ndipo mkazi wa Samisoni analira pamaso pake, nati, Ungondida, osandikonda; waphera anthu a mtundu wanga mwambi, osanditanthauzira ine. Ndipo ananena naye, Taona, sindinatanthauzira atate wanga kapena amai wanga, kodi ndikutanthauzire iwe? Ndipo analira pamaso pake masiku asanu ndi awiriwo pochitika madyerero ao; koma kunali kuti tsiku lachisanu ndi chiwiri anamuuza, popeza anamuumiriza; ndipo anatanthauzira anthu a mtundu wake mwambiwo. Ndipo amuna a pamudzi anati kwa Samisoni tsiku lachisanu ndi chiwiri, lisanalowe dzuwa, Chozuna choposa uchi nchiyani; ndi champhamvu choposa mkango nchiyani? Pamenepo ananena nao, Mukadapanda kulima ndi ng'ombe yanga, simukadatha kumasulira mwambi wanga. Ndipo mzimu wa Yehova unamgwera Samisoni, natsikira iye kwa Asikeloni, nawakantha amuna makumi atatu, natenga zovala zao, nawapatsa omasulira mwambiwo zovala zosinthanitsa. Koma adapsa mtima, nakwera kunka kunyumba ya atate wake. Ndipo mkazi wake wa Samisoni anakhala wa mnzake, amene adakhala bwenzi lake. Ndipo kunali atapita masiku, nyengo ya kucheka tirigu Samisoni anakacheza ndi mkazi wake ndi kumtengera mwanawambuzi, nati, Ndidzalowa kwa mkazi wanga kuchipinda. Koma atate wake sanamlole kulowamo. Nati atate wake, Ndinanenetsa kuti umuda konse, potero ndinampereka kwa bwenzi lako; mng'ono wake sakoma koposa iye nanga? Ukhale naye, m'malo mwa winayu. Koma Samisoni, ananena nao, Nthawi yino ndikhala wosapalamula pa Afilisti, powachitira choipa ine. Namuka Samisoni, nagwira ankhandwe mazana atatu, natenga miuni, nalunza michira, naika muuni pakati pa michira iwiri iliyonse. Nayatsa miuni, nawataya ku tirigu wosacheka wa Afilisti, natentha miulu, ndi tirigu wosacheka yemwe, ndi minda ya azitona yomwe. Pamenepo Afilisti anati, Wachita ichi ndani? Nati, Samisoni mkamwini wa munthuyo wa ku Timna, popeza analanda mkazi wake, nampereka kwa mnzake. Pamenepo Afilisti anakwera namtentha mkaziyo ndi atate wake ndi moto. Ndipo Samisoni ananena nao, Mukatero ndidzakubwezerani chilango ndi pamenepo ndidzaleka. Ndipo anawakantha nyung'unyu ndi ntchafu, makanthidwe akulu; natsika nakhala m'phanga mwa thanthwe la ku Etamu. Pamenepo Afilisti anakwera, namanga misasa m'Yuda, natandika m'Lehi. Ndipo anthu a Yuda anati, Mwatikwerera chifukwa ninji? Nati iwo, Takwera kumanga Samisoni, kumchitira iye monga anatichitira ife. Pamenepo anatsikira ku phanga la Etamu amuna zikwi zitatu a ku Yuda, nati kwa Samisoni, Sudziwa kodi kuti Afilisti ndiwo akutilamulira ife? Nchiyani ichi watichitira? Nati iye kwa iwowa, Monga anandichitira ine ndawachitira iwo. Ndipo ananena naye, Tatsika ife tikumange, kuti tikupereke m'dzanja la Afilisti, Nanena nao Samisoni, Mundilumbirire kuti simudzandigwera nokha. Ndipo anati kwa iye, Iai, koma kumanga tidzakumanga, ndi kukupereka m'dzanja lao; koma kupha sitikupha iwe. Nammanga iye ndi zingwe ziwiri zatsopano, nakwera naye kuchokera kuthanthwe. Pamene anafika ku Lehi Afilisti anafuula pokomana naye; koma mzimu wa Yehova unamgwera kolimba, ndi zingwe zokhala pa manja ake zinanga thonje lopserera ndi moto, ndi zomangira zake zinanyotsoka pa manja ake. Ndipo anapeza chibwano chatsopano cha bulu, natambasula dzanja lake nachigwira, nakantha nacho amuna chikwi chimodzi. Nati Samisoni, Ndi chibwano cha bulu, miulumiulu, amuna chikwi ndawakantha ndi chibwano cha bulu. Ndipo kunali, atatha kunena, anataya chibwano m'dzanja lake; nawatcha malowo Ramatilehi ndiko kunena chitunda cha chibwano. Ndipo anamva ludzu lambiri, naitana kwa Yehova, nati, Mwapatsa Inu chipulumutso ichi chachikulu ndi dzanja la kapolo wanu; ndipo kodi ndife nalo ludzu tsopano ndi kugwa m'dzanja la osadulidwa awa? Pamenepo Mulungu anang'amba pokumbika paja pa Lehi, natulukamo madzi; namwa iye, nubwera moyo wake, natsitsimuka iye; chifukwa chake anawatcha dzina lake, Kasupe wa wofuula, ndiwo m'Lehi mpaka lero lino. Ndipo Samisoni anaweruza Israele m'masiku a Afilisti zaka makumi awiri. Ndipo Samisoni anamuka ku Gaza, naonako mkazi wadama, nalowana naye. Koma wina anauza a ku Gaza, ndi kuti, Samisoni walowa kuno. Pamenepo anamzinga, namlalira usiku wonse pa chipata cha mudzi, nakhala chete usiku wonse ndi kuti, Tidikire mpaka kucha, pamenepo tidzamupha. Koma Samisoni anagona mpaka pakati pa usiku, nauka pakati pa usiku, nagwira zitseko za pa chipata cha mudzi, ndi mphuthu ziwirizo, nazichotsa ndi mpiringidzo womwe, naziika pa mapewa ake, nakwera nazo pamwamba pa phiri lili pandunji pa Hebroni. Ndipo pambuyo pake kunali kuti anakonda mkazi m'chigwa cha Soreki, dzina lake ndiye Delila. Ndipo akalonga a Afilisti anamkwerera mkaziyo, nanena naye, Umkope nuone umo muchokera mphamvu yake yaikulu, ndi umo tingakhoze kumtha khama, kuti timmange kumzunza; ndipo tidzakupatsa aliyense ndalama mazana khumi ndi limodzi. Pamenepo Delila anati kwa Samisoni, Ndikupempha, undiuze umo muchokera mphamvu yako yaikulu, ndi chimene angakumange nacho, kuti akuzunze. Nanena naye Samisoni, Akandimanga nazo nsinga zatsopano zisanu ndi ziwiri zosauma, ndidzakhala wofooka, wakunga munthu wina. Pamenepo akalonga a Afilisti anakwera nazo kwa mkaziyo nsinga zatsopano zisanu ndi ziwiri zosauma; ndipo iye anammanga nazo. Koma anali nao omlalira m'chipinda cha m'kati. Nanena naye, Afilisti akugwera, Samisoni. Pamenepo anadula nsingazi, monga iduka m'khosi yathonje pokhudza moto. M'mwemo mphamvu yake siinadziwike. Pamenepo Delila anati kwa Samisoni, Taona, wandipusitsa, ndi kundiuza mabodza; undiuze tsopano, ndikupempha, chimene angakumange nacho. Nanena naye, Akandimangitsa nazo zingwe zatsopano, zosagwira nazo ntchito pamenepo ndidzakhala wofooka wakunga munthu wina. Ndipo Delila anatenga nsinga zatsopano, nammanga nazo, nanena naye, Afilisti akugwera, Samisoni. Ndi omlalira analikulinda m'chipinda cha m'kati. Koma anazidula pa manja ake ngati thonje. Pamenepo Delila anati kwa Samisoni, Mpaka tsopano wandipusitsa, ndi kundiuza mabodza; undiuze chimene angakumange nacho. Nanena naye, Ukaomba njombi zisanu ndi ziwiri za pamutu panga mwa thonje loyala ndiko. Ndipo anachimanga ndi phanga, nati kwa iye, Akugwera Afilisti, Samisoni; nagalamuka iye patulo take, nazula phanga la pamtanda, ndi thonje loyala lomwe. Pamenepo ananena naye, Ukati bwanji, Ndikukonda, osamvana nane mtima wako? Wandipusitsa katatu tsopano, osandiuza umo muchokera mphamvu yako yaikulu. Ndipo kunali, popeza anamuumiriza masiku onse ndi mau ake, namkakamiza, moyo wake unavutika nkufuna kufa. Pomwepo anamfotokozera mtima wake wonse, nanena naye, Pamutu panga sipanapite lumo, pakuti ndine Mnaziri wa Mulungu chiyambire mimba ya mai wanga; akandimeta, mphamvu yanga idzandichokera, ndidzakhala wofooka wakunga munthu wina aliyense. Ndipo pamene Delila anaona kuti adamfotokozera mtima wake wonse, anatuma naitana akalonga a Afilisti, ndi kuti, Kwerani nthawi yino, pakuti wandifotokozera za mtima wake wonse. Nakwera akalonga a Afilisti nadza kwa iye nabwera nazo ndalamazo m'dzanja lao. Pamenepo anamgonetsa pa mabondo ake, naitana munthu, nameta njombi zake zisanu ndi ziwiri; nayamba kumzunza, nimchokera mphamvu yake. Ndipo anati, Afilisti akugwera, Samisoni. Nagalamuka iye m'tulo take, nati, Ndizituluka ngati nthawi zina, ndi kudzitakasika. Koma sanadziwe kuti Yehova adamchokera. Pamenepo Afilisti anamgwira, namkolowola maso, natsika naye ku Gaza, nammanga ndi maunyolo amkuwa; namperetsa m'kaidi. Koma atammetsa tsitsi la pamutu pake linayamba kumeranso. Ndipo anasonkhana akalonga a Afilisti kuperekera Dagoni mulungu wao nsembe yaikulu, ndi kusekerera; pakuti anati, Mulungu wathu wapereka Samisoni mdani wathu m'dzanja lathu. Ndipo pakumuona anthu analemekeza mulungu wao, pakuti anati, Mulungu wathu wapereka m'dzanja lathu mdani wathu, ndiye wakupasula dziko lathu, amene anatiphera ambiri. Ndipo kunali, pakukondwera mitima yao, anati, Kaitaneni Samisoni, atisewerere. Naitana Samisoni m'kaidi; nasewera iye pamaso pao; ndipo anamuka iye pakati pa mizati. Ndipo Samisoni anati kwa mnyamata womgwira dzanja, Ndileke, ndikhudze mizati imene nyumba ikhazikikapo, kuti nditsamirepo. Koma nyumbayi inadzala ndi amuna ndi akazi; ndi akalonga onse a Afilisti anali momwemo ndi patsindwi panali amuna ndi akazi ngati zikwi zitatu akuyang'ana pakusewera Samisoni. Pamenepo Samisoni anaitana kwa Yehova, nati, Yehova, Mulungu, mundikumbukire, ndikupemphani, ndi kundilimbitsa, ndikupemphani, nthawi yino yokha, Mulungu, kuti ndidzilipsiriretu tsopano apa Afilisti, chifukwa cha maso anga awiri. Ndipo Samisoni anagwira mizati iwiri ya pakati imene nyumba inakhazikikapo, natsamirapo wina ndi dzanja lamanja, ndi unzake ndi dzanja lamanzere. Nati Samisoni, Ndife nao Afilisti; nadziweramira mwamphamvu; ndipo nyumba idagwa pa akalonga, ndi pa anthu onse anali m'mwemo. Motero akufa amene anawapha pa kufa kwake anaposa amene anawapha akali moyo. Pamenepo anatsika abale ake ndi banja lonse la atate wake, namnyamula, nakwera naye, namuika pakati pa Zora ndi Esitaoli, m'manda a Manowa atate wake. Ndipo adaweruza Israele zaka makumi awiri. Ndipo ku mapiri a Efuremu kunali munthu dzina lake ndiye Mika. Ndipo iye anati kwa amai wake, Ndalama zija mazana khumi ndi limodzi anakuberani zimene munatembererapo, ndi kunenanso m'makutu mwanga, taonani ndalamazo ndili nazo, ndinazitenga ndine. Pamenepo amai wake anati, Yehova adalitse mwana wanga. Nabwezera amake ndalama zija mazana khumi ndi limodzi; nati amai wake, Kupatula ndapatulira Yehova ndalamazo zichoke ku dzanja langa, zimuke kwa mwana wanga, kupanga nazo fano losema ndi fano loyenga; m'mwemo ndikubwezera izi. Ndipo pamene anambwezera mai wake ndalamazo, mai wake anatapako ndalama mazana awiri, nazipereka kwa woyenga, ndiye anazipanga fano losema ndi fano loyenga; ndipo linakhala m'nyumba ya Mika. Koma munthuyu Mika anali nayo nyumba ya milungu, napanga chovala cha wansembe, ndi timafano, namninkha zansembe mwana wake wina wamwamuna, amene anakhala wansembe wake. Masikuwa panalibe mfumu m'Israele, yense anachita chomuyenera m'maso mwake. Ndipo panali mnyamata wa ku Betelehemu-Yuda wa banja la Yuda, ndiye Mlevi, nagonera iye komweko. Adachokera munthuyo m'mudzi m'Betelehemu-Yuda, kugonera paliponse akapeza pokhala; ndi pa ulendo wake anafika ku mapiri a Efuremu, kunyumba ya Mika. Ndipo Mika ananena naye, Ufumira kuti? Nati kwa iye, Ndine Mlevi wa ku Betelehemu-Yuda, ndilikumuka kugonera kumene ndikapeza pokhala. Nanena naye Mika, Khalitsa nane, nukhale atate wanga, ndi wansembe wanga, ndipo ndidzakupatsa ndalama khumi pachaka, ndi chovala chofikira, ndi zakudya zako. Nalowa Mleviyo. Ndi Mleviyo anavomera kukhalitsa ndi munthuyo; ndi mnyamatayo anamkhalira ngati mmodzi wa ana ake. Ndipo Mika anamninkha zansembe Mleviyo, ndi mnyamatayo anakhala wansembe wake, nakhala m'nyumba ya Mika. Nati Mika, Tsopano ndidziwa kuti Yehova adzandichitira chokoma, popeza ndili naye Mlevi akhale wansembe wanga. Masiku ajawo panalibe mfumu m'Israele; masiku ajanso fuko la Adani anadzifunira cholowa chakukhalako; pakuti kufikira tsiku lija sichinawagwera cholowa chao pakati pa mafuko a Israele. Ndipo ana a Dani anatuma a banja lao amuna asanu a mwa iwo onse, anthu olimba mtima, a ku Zora, ndi a ku Esitaoli, kuzonda dziko ndi kufunafunamo; nanena nao, Mukani, mufunefune m'dziko. Nafika iwo ku mapiri a Efuremu kunyumba ya Mika, nagona komweko. Pokhala iwo m'nyumba ya Mika, anazindikira mau a mnyamata Mleviyo, napatukirako, nanena naye, Anadza nawe kuno ndani? Uchitanji muno? Ukhala nacho chiyani kuno? Ndipo ananena nao, Mika anandichitira chakutichakuti, napangana nane za ntchito, ndipo ndikhala wansembe wake. Pamenepo ananena naye, Utifunsire kwa Mulungu, kuti tidziwe ngati ulendo wathu timukawo udzakoma. Nanena nao wansembeyo, Mukani mumtendere, ulendo wanu muyendawo uli pamaso pa Yehova. Pamenepo amuna asanuwa anachoka, nafika ku Laisi; naona anthu anali m'mwemo, kuti anakhala okhazikika mtima, monga anakhala Asidoni, odekha ndi osatekeseka; popeza m'dzikomo munalibe mwini bwalo wakuchititsa manyazi m'chinthu chilichonse; nasiyana kutali ndi Asidoni, ndipo analibe kanthu ndi munthu aliyense. Ndipo asanuwo anafikanso kwa abale ao ku Zora ndi Esitaoli; ndi abale ao ananena nao, Mutani inu? Nati iwo, Taukani, tiwakwerere; pakuti tapenya dziko, ndipo taonani, ndilo lokoma ndithu; ndi inu muli chete kodi? Musamachita ulesi kumuka ndi kulowa kulandira dzikolo. Pomuka inu mudzafikira anthu okhazikika mtima ndi dziko lachitando; pakuti Mulungu walipereka m'dzanja lanu; pamenepo mposasowa kanthu kalikonse kali pa dziko lapansi. Pamenepo amuna mazana asanu ndi limodzi, omangira zida za nkhondo m'chuuno, anaphumulako a banja la a Dani, anachokera ku Zora, ndi ku Esitaoli. Nakwera namanga misasa m'Kiriyati-Yearimu, m'Yuda; chifukwa chake anatcha dzina lake la malowo chigono cha Dani, mpaka lero; taona, ali m'tseri mwa Kiriyati-Yearimu. Ndipo anapitirira komweko kunka ku mapiri a Efuremu, nadza kunyumba ya Mika. Pamenepo anayankha amuna asanu anamukawo kukazonda dziko la Laisi, nanena ndi abale ao, Kodi mudziwa kuti m'nyumba izi muli chovala cha wansembe, ndi timafano ndi fano losema, ndi fano lonyenga? Ndipo tsopano dziwani choyenera inu kuchita. Napatuka iwo kumkako, nafika kunyumba ya mnyamata Mleviyo, ndiyo nyumba ya Mika, namfunsa ngati ali bwanji. Ndipo amuna mazana asanu ndi limodzi omangira zida zao za nkhondo m'chuuno, ndiwo a ana a Dani, analikuima polowera pa chipata; koma amuna asanu omukawo kukazonda dziko anakwera analowako, natenga fano losema, ndi chovala cha wansembe ndi timafano, ndi fano loyenga; ndi wansembe anaima polowera pa chipata pamodzi ndi amuna mazana asanu ndi limodzi omangira zida za nkhondo m'chuuno. Atalowa iwo m'nyumba ya Mika, natengako fano losema, chovala cha wansembe, ndi timafano, ndi fano loyenga, wansembeyo ananena nao, Muchitanji? Ndipo ananena naye, Khala chete, tseka pakamwa pako, numuke nafe, nutikhalire atate ndi wansembe wathu; chikukomera nchiti, kukhala wansembe wa nyumba ya munthu mmodzi, kapena kukhala wansembe wa fuko ndi banja m'Israele? Nukondwera mtima wa wansembeyo, natenga iye chovala cha wansembe, ndi timafano ndi fano losema, nalowa pakati pa anthu. Atatero anabwerera, nachoka, natsogoza ana ang'ono ndi zoweta ndi akatundu. Atafika kutali ndi nyumba ya Mika, Mikayo anawamemeza amuna a m'nyumba zoyandikizana ndi yake, natsata ndi kuwapeza ana a Dani. Ndipo anafuula kwa ana a Dani. Nacheuka iwo nati kwa Mika, Chakusowa chiyani, kuti wamemeza anthu ako? Nati iye, Mwanditengera milungu yanga ndinaipanga, ndi wansembe, ndi kuchoka; chinditsaliranso chiyani? Ndipo muneneranji kwa ine, Chakusowa nchiyani? Koma ana a Dani anati kwa iye, Mau ako asamveke ndi ife, angakugwere anthu owawa mtima, nukataya moyo wako ndi wa iwo a m'nyumba mwako. Nayenda ulendo wao ana a Dani; ndipo Mika pakuona kuti anamposa mphamvu, anatembenuka nabwerera kunyumba kwake. M'mwemo anatenga zimene Mika adachipanga, ndi wansembe anali naye, nafika ku Laisi, kwa anthu odekha ndi okhazikika mtima, nawakantha ndi lupanga lakuthwa, natentha mudzi wao ndi moto. Ndipo panalibe wolanditsa, popeza ku Sidoni nkutali, ndipo analibe kuyenderana ndi anthu ena; ndiko ku chigwa chokhala ku Beterehobu. Pamenepo anamanganso mudziwo, nakhala m'mwemo. Ndipo analitcha dzina la mudziwo Dani, kutsata dzina la atate wao Dani wombala Israele; koma poyambapo dzina la mudzi linali Laisi. Ndipo ana a Dani anadziimitsira fano losemalo; ndi Yonatani mwana wa Geresomo mwana wa Manase, iye ndi ana ake amuna anali ansembe a fuko la Adani mpaka tsiku lija anatenga ndende anthu a m'dziko. Motero anadziikira fano losema la Mika, limene adalipanga, masiku onse okhala nyumba ya Mulungu ku Silo. Ndipo kunali, masiku aja, pamene panalibe mfumu m'Israele, panali munthu Mlevi wogonera kuseri kwa mapiri a Efuremu amene anadzitengera mkazi wamng'ono wa ku Betelehemu-Yuda. Koma mkazi wake wamng'ono anachita chigololo akali naye, namchokera kunka kunyumba ya atate wake ku Betelehemu-Yuda, nakhalako nthawi ya miyezi inai. Koma anauka mwamuna wake namtsata kukamba naye zamtima, kumbwezanso; napita ndi mnyamata wake, ndi abulu awiri. Ndipo mkaziyo anadza naye kunyumba ya atate wake. Ndipo pakumuona atate wa mkaziyo anakondwera kukomana naye. Ndipo mpongozi wake, ndiye atate wa mkaziyo, anamuimika kuti akhale naye masiku atatu; nadya namwa nagona komweko. Ndipo kunali, tsiku lachinai, analawirira mamawa, nanyamuka iye kuchoka; koma atate wa mkaziyo anati kwa mkamwini wake, Limbitsa mtima wako ndi mkate pang'ono, ndipo utatero upite. Nakhala pansi nadya namwa onse awiri pamodzi; nati kwa munthuyo atate wa mkaziyo, Uvomere, ugone kuno usiku, nusekerere mtima wako. Ndipo munthuyo ananyamuka kuti amuke; koma mpongozi wakeyo anamkakamiza, nagonanso komweko. Nalawirira mamawa tsiku lachisanu kuti amuke, koma atate wa mkaziyo anati, Ulimbitse mtima wako, nulindire lipendeke dzuwa; nadya iwo onse awiri. Pamenepo munthuyo ananyamuka kuchoka, iye ndi mkazi wake wamng'ono ndi mnyamata wake; koma mpongozi wake, atate wa mkaziyo, ananena naye, Tapenya, lapendeka dzuwa, ugone kuno usiku; tapenya lapendekatu dzuwa, ugone kuno, nusekerere mtima wako; nimulawire mamawa kunka ulendo wanu kwanu. Koma munthuyo anakana kugonako usiku, nanyamuka, nachoka, nadza pandunji pa Yebusi (ndiwo Yerusalemu); ndi pamodzi naye panali abulu awiri omangirira mbereko; anali nayenso mkazi wake wamng'ono. Pofika iwo pa Yebusi linalimkulowa dzuwa, ndi mnyamata anati kwa mbuye wake, Tiyeni, tipatukire mudzi uwu wa Ayebusi ndi kugona pomwepa. Koma mbuye wake ananena naye, Tisapatukire mudzi wachilendo, wosati wa ana a Israele, koma tipitirire kunka ku Gibea. Nati kwa mnyamata wake, Tiyeni, tiyandikire kwinako: tigone m'Gibea, kapena m'Rama. Napitirira iwo, nayenda, ndi dzuwa linawalowera pafupi pa Gibea, ndiwo wa Benjamini. Napatukirako, kuti alowe nagone ku Gibea; nalowa iye, nakhala pansi m'khwalala la mudziwo, pakuti panalibe wina wowalandira m'nyumba agonemo, wakuwapatsa pogona. Ndipo taonani, munthu nkhalamba anachokera ku ntchito yake kumunda madzulo; munthuyu ndiye wa ku mapiri a Efuremu, nagonera ku Gibea; koma anthu pamenepo ndiwo Abenjamini. Pamene anakweza maso ake anaona munthu wa pa ulendoyo m'khwalala la mudzi; ndi nkhalambayo inati, Umuka kuti? Ufumira kuti? Ndipo ananena nayo, Tili kuchokera ku Betelehemu-Yuda, kunka ku mbali za mapiri a Efuremu, ndiko ndifumira ine; koma ndidamuka ku Betelehemu-Yuda; ndipo tsopano ndili kumuka kunyumba ya Yehova; koma palibe munthu wondipatsa nyumba. Ngakhale udzu ndi chakudya cha abulu athu ziliko; ndi mkate ndi vinyo zilikonso kwa ine ndi kwa mdzakazi wako ndi kwa mnyamata wokhala ndi akapolo ako; kosasowa kanthu. Ndipo nkhalambayo inati, Mtendere ukhale ndi iwe, komatu, zosowa zako zonse ndidzakupatsa ndi ine; pokhapo usagone m'khwalala. Pamenepo anamlonga m'nyumba yake, napatsa abulu chakudya; ndipo iwo anasamba mapazi ao, nadya, namwa. Pokondweretsa iwo mitima yao, taonani amuna a m'mudziwo, ndiwo anthu otama zopanda pake, anazinga nyumba, nagogodagogoda pachitseko; nati kwa mwini nyumba nkhalambayo ndi kuti, Tulutsa mwamunayo adalowa m'nyumba mwako kuti timdziwe. Ndipo munthu mwini nyumba anawatulukira nanena nao, Iai, abale anga, musachite choipa chotere; popeza mwamuna uyu walowa m'nyumba mwanga, musachite chopusa ichi. Taonani, mwana wanga wamkazi ndiye namwali, ndi mkazi wake wamng'ono siwa; ndiwatulutse iwo, muwachepetse iwo, ndi kuwachitira monga muyesa chokoma; koma mwamuna uyu musamchitire chopusa ichi. Koma amunawo sanafune kumvera; motero munthuyu anagwira mkazi wake wamng'ono, natuluka naye kwa iwo kunja; namdziwa iwo, nachita naye zoipa usiku wonse mpaka m'mawa; namlola achoke mbandakucha. Nadza mkaziyo, kutacha, nagwa pakhomo pa nyumba ya munthu padali mbuye wake, kufikira kutayera. Pamene mbuye wake anauka mamawa, natsegula pakhomo pa nyumba, natuluka kunka ulendo wake, taona, mkazi wake wamng'ono, atagwa pakhomo pa nyumba ndi manja ake pachiundo. Ndipo ananena naye, Tauka, timuke; koma panalibe womyankha. Pamenepo anamuika pa bulu; nanyamuka mwamunayo, namka kwao. Ndipo pofika iye kunyumba kwake, anatenga mpeni, nagwira mkazi wake wamng'onoyo namgawa chiwalochiwalo magawo khumi ndi awiri, namtumiza ku malire onse a Israele. Ndipo kunali kuti onse amene anachiona anati, Sichinachitika, inde sichinaoneka chotere chiyambire tsiku lokwera ana a Israele kutuluka m'dziko la Ejipito mpaka lero lino; lingiriranipo, mupangane nzeru, nimunene. Pamenepo anatuluka ana onse a Israele, nuunjikana msonkhano kwa Yehova ku Mizipa ngati munthu mmodzi, kuyambira ku Dani mpaka Beereseba ndi dziko la Giliyadi lomwe. Ndipo akulu a anthu onse a mafuko onse a Israele anadziimika mu msonkhano wa anthu a Mulungu, anthu oyenda pansi zikwi mazana anai akusolola lupanga. Ndipo ana a Benjamini anamva kuti ana a Israele adakwera kunka ku Mizipa. Nati ana a Israele, Nenani, choipa ichi chinachitika bwanji? Ndipo Mlevi, mwamuna wa mkazi anaphedwayo, anayankha nati, Ndinadza ine ku Gibea wa Benjamini, ine ndi mkazi wanga wamng'ono, kugonako. Nandiukira eni ake a Gibea, nandizingira nyumba usiku; nafuna kundipha ine, namchitira choipa mkazi wanga wamng'ono, nafa iye. Pamenepo ndinagwira mkazi wanga wamng'ono ndi kumgawa ndi kumtumiza m'dziko lonse la cholowa cha Israele, pakuti anachita chochititsa manyazi ndi chopusa m'Israele. Taonani, inu nonse, ndinu ana a Israele, mudzinenere mau ndi kudzipangira nokha kuno. Ndipo anthu onse anauka ngati munthu mmodzi, ndi kuti, Palibe mmodzi wa ife adzamuka kuhema kwake, kapena kupatukira nyumba yake, koma tsopano ichi ndicho tidzachitira Gibea: tidzaukwerera ndi kulota maere. Ndipo tidzatapa amuna khumi limodzi pa zana limodzi, mwa mafuko onse a Israele; ndi zana limodzi pa zikwi chimodzi, ndi chikwi chimodzi pa zikwi khumi kutengera anthu kamba; kuti pakufika ku Gibea wa Benjamini, auchitire monga mwa chopusa chonse unachita m'Israele. Potero amuna onse a Israele anasonkhanira mudziwo, olunzika ngati munthu mmodzi. Ndipo mafuko a Israele anatuma anthu mwa fuko lonse la Benjamini, ndi kuti, Choipa chanji ichi chinachitika mwa inu? Ndipo tsopano perekani amunawo otama zopanda pake, okhala m'Gibea, kuti tiwaphe, ndi kuchotsera Israele choipachi. Koma Benjamini sanafune kumvera mau a abale ao, ana a Israele. Ndipo ana a Benjamini anasonkhana kuchokera kumidzi kunka ku Gibea, kuti atuluke kulimbana ndi ana a Israele. Ndipo anawerenga ana a Benjamini a m'midzi tsiku lija amuna zikwi makumi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi akusolola lupanga; osawerenga okhala m'Gibea, ndiwo amuna osankhika mazana asanu ndi awiri. Mwa anthu awa onse munali amuna osankhika mazana asanu ndi awiri amanzere, yense wa iwo amaponya mwala mwa maluli osaphonya. Ndipo anawerenga amuna a Israele, osati Benjamini, amuna zikwi mazana anai osolola lupanga, anthu a nkhondo okhaokha. Nauka ana a Israele, nakwera kunka ku Betele, nafunsira kwa Mulungu, nati, Ayambe ndani kutikwerera pa ana a Benjamini? Ndipo Yehova anati, Ayambe ndi Yuda. Nauka ana a Israele m'mawa, naumangira Gibea misasa. Ndipo amuna a Israele anatuluka kulimbana ndi Benjamini; ndi amuna a Israele anawandandalikira nkhondo ku Gibea. Pamenepo ana a Benjamini anatuluka m'Gibea, naononga a Israele tsiku lija zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, kuwagoneka pansi. Koma anthu, ndiwo amuna a Israele, anadzilimbitsa nanikanso nkhondo kumene anandandalika tsiku loyambalo. Ndipo ana a Israele anakwera nalira misozi pamaso pa Yehova mpaka madzulo; nafunsira kwa Yehova ndi kuti, Ndiyandikizenso kodi kulimbana nkhondo ndi ana a Benjamini mbale wanga? Ndipo Yehova anati, Mumkwerere. Potero ana a Israele anayandikira ana a Benjamini m'mawa mwake. Ndipo Benjamini anawatulukira ku Gibea m'mawa mwake, naononganso a ana a Israele amuna zikwi khumi ndi zisanu ndi zitatu kuwagoneka pansi; ndiwo onse osolola lupanga. Pamenepo ana onse a Israele ndi anthu onse anakwera nafika ku Betele, nalira misozi, nakhala pansi pomwepo pamaso pa Yehova, nasala chakudya tsiku lomwelo mpaka madzulo; napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika pamaso pa Yehova. Ndipo ana a Israele anafunsira kwa Yehova; pakuti likasa la chipangano la Mulungu linakhala komweko masiku aja, namaima ku likasalo Finehasi mwana wa Eleazara mwana wa Aroni, masiku aja; nati, Kodi nditulukenso kulimbana nkhondo ndi ana a Benjamini mbale wanga, kapena ndileke? Ndipo Yehova anati, Kwerani, pakuti mawa ndidzampereka m'dzanja lako. Ndipo Israele anaika olalira Gibea pozungulira pake. Ndipo ana a Israele anakwerera ana a Benjamini tsiku lachitatu, nanika pa Gibea monga nthawi zina. Natuluka ana a Benjamini kukomana ndi anthuwo, nakokedwa kutali ndi mudzi, nayamba kuwakantha ndi kuwapha anthu amuna a Israele, ngati makumi atatu monga nthawi zina, m'makwalala, limodzi la awo lokwera kunka ku Betele, ndi lina ku Gibea kuthengo. Ndipo ana a Benjamini anati, Tawakantha pamaso pathu monga poyamba paja. Koma ana a Israele anati, Tithawe, tiwakokere kutali ndi mudzi kumakwalala. Nauka amuna onse a Israele m'malo ao nanika ku Baala-Tamara; natuluka Aisraele olalira aja m'malo mwao, kumwera kwa Geba. Ndipo anadza pandunji pa Gibea amuna osankhika m'Israele monse zikwi khumi, nikula nkhondo; koma sanadziwe kuti choipa chili pafupi kuwakhudza. Ndipo Yehova anakantha Benjamini pamaso pa Israele; ndi ana a Israele anawaononga a Benjamini tsiku lija amuna zikwi makumi awiri ndi zisanu, kudza zana limodzi; awa onse ndiwo akusolola lupanga. Ndipo ana a Benjamini anaona kuti takanthidwa; popeza amuna a Israele anawapatsa Abenjamini malo, pakuti anatama olalira amene anawaikiratu pa Gibea. Nafulumira olalirawo nathamangira Gibea, nabalalika olalirawo, nakantha mudzi wonse ndi lupanga lakuthwa. Koma kunali chizindikiro choikika pakati pa amuna a Israele ndi olalirawo, ndicho chakuti afukitse mtambo wa utsi kumudzi. Ndi nkhondo ya Israele inathawa, ndipo Benjamini anayamba kuwakantha ndi kuwagwaza amuna a Israele, ngati amuna makumi atatu, pakuti anati, Ndithu tawakantha konse pamaso pathu, monga ku nkhondo yoyambayo. Koma pamene mtambo unayamba kukwera m'mudzi ngati utsi uli tolo, Abenjamini anacheuka, ndipo taonani, pamodzi ponse panafuka utsi kumwamba. Natembenuka amuna a Israele; nadabwa amuna a Benjamini; popeza anaona kuti chidawagwera choipa. Nabwerera iwo pamaso pa amuna a Israele kunka njira ya chipululu; koma nkhondo inawalondetsa; ndi aja otuluka m'mudzi anawaononga pakati pao. Anawazinga Abenjamini, anawapirikitsa, nawapondereza pampumulo mpaka pandunji pa Gibea, kotulukira dzuwa. Ndipo adagwa a Benjamini amuna zikwi khumi ndi zisanu ndi zitatu; iwo onse ndiwo ngwazi. Natembenuka iwo, nathawira kuchipululu ku thanthwe la Rimoni; koma anawakunkha m'makwalala amuna zikwi zisanu; nawalondetsa ku Gidomu, nakantha a iwowa amuna zikwi ziwiri. Potero onse amene adagwa a Benjamini tsiku lija, ndiwo amuna zikwi makumi awiri mphambu zisanu, akusolola lupanga; iwo onse ndiwo ngwazi. Koma amuna mazana asanu ndi limodzi anabwerera nathawira kuchipululu, ku thanthwe la Rimoni, nakhala m'thanthwe la Rimoni miyezi inai. Ndipo amuna a Israele anabwereranso kwa ana a Benjamini, nawakantha ndi lupanga lakuthwa a m'mudzi wonse, ndi zoweta, ndi zonse adazipeza; anatenthanso midzi yonse anaipeza. Koma amuna a Israele adalumbira ku Mizipa, ndi kuti, Palibe mmodzi wa ife adzapereka mwana wake wamkazi kwa Mbenjamini akhale mkazi wake. Ndipo anthu anadza ku Betele, nakhala pansi pomwepo pamaso pa Mulungu mpaka madzulo; nakweza mau ao ndi kulira misozi yambiri. Nati iwo, Yehova Mulungu wa Israele, chachitika ichi chifukwa ninji m'Israele, kuti lasowa lero fuko limodzi m'Israele? Ndipo kunali m'mawa mwake, anthu analawirira mamawa namangako guwa la nsembe, napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika. Nati ana a Israele, Ndani iye mwa mafuko onse a Israele amene sanakwere kudza kumsonkhano kwa Yehova? Pakuti panali lumbiro lalikulu pa iye wosakwera kudza kwa Yehova ku Mizipa, ndi kuti, Aphedwe ndithu. Ndipo ana a Israele anamva chifundo chifukwa cha Benjamini mbale wao, nati, Fuko limodzi lalikhidwa pa Israele leroli. Tidzatani kuwafunira otsalawo akazi, popeza tinalumbira ife pa Yehova kuti sitidzawapatsa ana athu akazi akhale akazi ao? Nati iwo, Kodi pali lina la mafuko a Israele losakwera kudza kwa Yehova ku Mizipa? Ndipo taonani, kuchokera ku Yabesi-Giliyadi sanadze mmodzi kumisasa, kumsonkhano. Pakuti pamene anawerenga anthu, taonani, panalibe mmodzi komweko wa okhala m'Yabesi-Giliyadi. Ndipo msonkhano unatumizako amuna zikwi khumi ndi ziwiri, ndiwo ngwazi, nawalamulira ndi kuti, Mukani, nimuwakanthe okhala m'Yabesi-Giliyadi ndi lupanga lakuthwa, ndi akazi ndi ana ang'ono. Ndipo chimene mukachite ndi ichi: mukaononge konse mwamuna aliyense, ndi mkazi aliyense wodziwa mwamuna mogona naye. Ndipo anapeza mwa anthu a Yabesi-Giliyadi anamwali mazana anai osadziwa mwamuna mogona naye; nabwera nao kumisasa ku Silo, ndiwo a m'dziko la Kanani. Ndipo msonkhano wonse unatumiza mau kwa ana a Benjamini okhala m'thanthwe la Rimoni, nawalalikira mtendere. Nakwera Abenjamini nthawi ija, ndipo anawapatsa akazi amene anawasunga amoyo mwa akazi a Yabesi-Giliyadi; koma sanawafikire. Ndipo anthu anamva chifundo pa Benjamini, pakuti Yehova adang'amba mafuko a Israele. Pamenepo akulu a msonkhano anati, Tidzatani, kuwafunira akazi otsalawo, popeza akazi anatha psiti m'Benjamini? Nati iwo, Pakhale cholowa cha iwo opulumuka a Benjamini, lingafafanizidwe fuko m'Israele. Koma sitikhoza ife kuwapatsa ana athu akazi akhale akazi ao; pakuti ana a Israele adalumbira ndi kuti, Atembereredwe wakupatsa Abenjamini mkazi. Nati iwo, Taonani, pali madyerero a Yehova chaka ndi chaka ku Silo, ndiko kumpoto kwa Betele, kum'mawa kwa mseu wokwera kuchokera ku Betele kunka ku Sekemu, ndi kumwera kwa Lebona. Ndipo analamulira ana a Benjamini ndi kuti, Mukani, mulalire m'minda yamphesa; nimuyang'ane, ndipo taonani, atatuluka ana akazi a Silo kuvinavina, pamenepo mutuluke m'minda yamphesa ndi kudzigwirira yense mkazi wake mwa ana akazi a Silo, ndi kumuka naye ku dziko la Benjamini. Ndipo kudzali, akatifikira atate ao kapena alongo ao kunena nafe mlandu, tidzanena nao, Mutipatse awa, pakuti sitinawatengera yense mkazi wake kunkhondo; pakuti inunso simunawaninkha awa; mukadatero mukadapalamula tsopano. Nachita chotere ana a Benjamini, nadzitengera akazi monga mwa kuwerenga kwao, a ovina aja, amene anawatenga mwachifwamba; namuka iwo nabwerera ku cholowa chao, namanga midzi, nakhalamo. Ndipo ana a Israele anachokako nthawi ija yense kunka ku fuko lake, ndi banja lake, natulukako yense kunka ku cholowa chake. Panalibe mfumu m'Israele masiku aja; yense anachita chomkomera pamaso pake. Ndipo masiku akuweruza oweruzawo munali njala m'dziko. Ndipo munthu wa ku Betelehemu-Yuda anamuka nakagonera m'dziko la Mowabu, iyeyu, ndi mkazi wake, ndi ana ake amuna awiri. Dzina la munthuyo ndiye Elimeleki, ndi dzina la mkazi wake ndiye Naomi, ndi maina a ana ake awiri ndiwo Maloni, ndi Kilioni; ndiwo Aefurati a ku Betelehemu-Yuda. Iwowa ndipo analowa m'dziko la Mowabu, nakhala komweko. Ndipo Elimeleki mwamuna wake wa Naomi anamwalira; natsala iye ndi ana ake awiri. Nadzitengera iwo akazi a ku Mowabu; wina dzina lake ndiye Oripa, mnzake dzina lake ndiye Rute; ndipo anagonera komweko ngati zaka khumi. Koma Maloni ndi Kilioni anamwalira onse awiri; motero ana ake amuna awiri ndi mwamuna wake anamsiya mkaziyo. Pamenepo ananyamuka iyeyu ndi apongozi ake kuti abwerere kuchoka m'dziko la Mowabu; pakuti adamva m'dziko la Mowabu kuti Yehova adasamalira anthu ake ndi kuwapatsa chakudya. Natuluka iye kumene anakhalako ndi apongozi ake awiri pamodzi naye; namka ulendo wao kubwerera ku dziko la Yuda. Ndipo Naomi anati kwa apongozi ake awiri, Mukani, bwererani yense wa inu kunyumba ya amai wake; Yehova akuchitireni zokoma, monga umo munachitira akufa aja ndi ine. Yehova akuloleni mupeze mpumulo yense m'nyumba ya mwamuna wake. Nawapsompsona, nakweza iwo mau ao nalira misozi. Ndipo ananena naye, Iai, koma tidzapita nanu kwa anthu a kwanu. Nati Naomi, Bwererani, ana anga, mudzatsagana nane bwanji? Ngati ndili nao m'mimba mwanga ana amuna ena kuti akhale amuna anu? Bwererani, ana anga, mukani, pakuti ndakalambitsa ine, sindikhoza kukhala naye mwamuna. Ngakhale ndikati, Ndili nacho chiyembekezo, ndikhala naye mwamuna usiku uno, ndi kubalanso ana amuna; kodi mudzawalindirira akakula? Mudzadziletsa osakwatibwa? Iai, ana anga, pakuti chandiwawa koposa chifukwa cha inu popeza dzanja la Yehova landitulukira. Nakweza iwo mau ao, naliranso misozi; ndi Oripa anampsompsona mpongozi wake, koma Rute anamkangamira. Pamenepo anati, Taona mbale wako wabwerera kwa anthu a kwao, ndi kwa mulungu wake, bwerera umtsate mbale wako. Nati Rute, Musandiumirize kuti ndikusiyeni, ndi kubwerera osakutsatani; pakuti kumene mumukako ndimuka inenso, ndi kumene mugonako ndigona inenso; anthu a kwanu ndiwo anthu a kwa inenso, ndi Mulungu wanu ndiye Mulungu wanga; kumene mudzafera inu ine ndidzafera komweko, ndi kuikidwa komweko; andilange Yehova naonjezeko, chilichonse chikasiyanitsa inu ndi ine, koma imfa ndiyo. Ndipo pakuona kuti analimbika kumuka naye, analeka kulankhula naye. Namuka iwo awiriwo mpaka anafika ku Betelehemu. Ndipo kunali pakufika iwo ku Betelehemu, mudzi wonse unapokosera za iwo; nati, Kodi uyu ndi Naomi? Koma ananena nao, Musanditcha Naomi, munditche Mara; pakuti Wamphamvuyonse anandichitira zowawa ndithu. Ndinachoka pano wolemera, nandibwezanso kwathu Yehova wopanda kanthu; munditcheranji Naomi, popeza Yehova wandichitira umboni wakunditsutsa, ndi Wamphamvuyonse wandichitira chowawa? Momwemo anabwera Naomi ndi Rute Mmowabu mpongozi wake pamodzi naye, amene anabwera kuchokera ku dziko la Mowabu; ndipo anafika ku Betelehemu, pakuyamba anthu kucheka barele. Ndipo Naomi anali naye mbale wa mwamuna wake, ndiye munthu mwini chuma chambiri wa banja la Elimeleki; dzina lake ndiye Bowazi. Nati Rute Mmowabu kwa Naomi, Mundilole ndimuke kumunda, ndikatole khunkha la ngala za tirigu, kumtsata iye amene adzandikomera mtima. Nanena naye, Muka, mwana wanga. Namuka iye, nakatola khunkha m'munda namatsata ochekawo; ndipo kudangotero naye kuti deralo la munda linali la Bowazi, ndiye wa banja la Elimeleki. Ndipo taona, Bowazi anafuma ku Betelehemu, nati kwa ocheka, Yehova akhale nanu. Namyankha iwo, Yehova akudalitseni. Nati Bowazi kwa mnyamata woyang'anira ochekawo, Mkazi uyu ngwa yani? Ndipo mnyamata woyang'anira ochekawo anayankha nati, Ndiye mkazi Mmowabuyo anabwera ndi Naomi ku dziko la Mowabu; ndipo anati, Undilole, ndikunkhe ndiole pakati pa mitolo potsata ochekawo; nadza iye nakhalakhala kuyambira m'mawa mpaka tsopano; koma m'nyumba samakhalitsamo. Pamenepo Bowazi ananena ndi Rute, Ulikumva, mwana wanga? Usakakhunkha m'munda mwina, kapena kupitirira pano, koma uumirire adzakazi anga mommuno. Maso ako akhale pa munda achekawo, ndi kuwatsata; kodi sindinawauza anyamata asakukhudze? Ndipo ukamva ludzu, muka kumitsuko, ukamweko otunga anyamatawo, Potero anagwa nkhope yake pansi, nadziweramira pansi, nanena naye, Mwandikomera mtima chifukwa ninji kuti mundisamalira ine, popeza ndine mlendo? Ndipo Bowazi anayankha nanena naye, Anandifotokozera bwino zonse unachitira mpongozi wako atafa mwamuna wako; ndi kuti wasiya atate wako ndi amai ako, ndi dziko lobadwirako iwe, ndi kudza kwa anthu osawadziwa iwe kale. Yehova akubwezere ntchito yako, nakupatse mphotho yokwanira Yehova, Mulungu wa Israele, amene unadza kuthawira pansi pa mapiko ake. Nati iye, Mundikomere mtima mbuye wanga, popeza mwandisangalatsa, popezanso mwanena chokondweretsa mtima wa mdzakazi wanu, ndingakhale ine sindine ngati mmodzi wa adzakazi anu. Ndipo pa nthawi ya kudya Bowazi ananena naye, Sendera kuno, nudyeko mkate; nusunse nthongo yako m'vinyo wosasayo. Nakhala iye m'mbali mwa ochekawo; ndipo anamtambasulira dzanja kumninkha tirigu wokazinga, nadya iye, nakhuta, nasiyapo. Ndipo ataumirira kukatola khunkha, Bowazi analamulira anyamata ake ndi kuti, Atole khunkha ngakhale pakati pa mitolo, musamchititse manyazi. Ndiponso mumtayire za m'manja, ndi kuzisiya, natole khunkha, osamdzudzula. Natola khunkha iye m'munda mpaka madzulo; naomba khunkhalo; napeza ngati efa wa barele, nalisenza nalowa kumudzi; ndipo mpongozi wake anaona khunkhalo; Rute natulutsanso nampatsa mkute uja anausiya atakhuta. Ndipo mpongozi wake ananena naye, Unakatola kuti khunkha lero? Ndi ntchito udaigwira kuti? Adalitsike iye amene anakusamalira. Ndipo anamfotokozera mpongozi wake munthu amene anakagwirako ntchito, nati, Dzina lake la munthuyo ndinakagwirako ntchito lero ndiye Bowazi. Nati Naomi kwa mpongozi wake, Yehova amdalitse amene sanaleke kuwachitira zokoma amoyo ndi akufa. Ndipo Naomi ananena naye, Munthuyo ndiye mbale wathu, ndiye mmodzi wa iwo otiombolera cholowa. Ndipo Rute Mmowabu anati, Ananenanso nane ndithu, Uwaumirire anyamata anga, mpaka atatha kucheka zanga zonse za m'minda. Nati Naomi kwa Rute mpongozi wake, Nchabwino, mwana wanga, kuti uzituluka nao adzakazi ake, ndi kuti asakukomane m'munda wina uliwonse. Momwemo anaumirira adzakazi a Bowazi kuti atole khunkha kufikira atatha kucheka barele ndi tirigu; ndipo anakhala iye kwao kwa mpongozi wake. Pamenepo Naomi mpongozi wake ananena naye, Mwana wanga, kodi ndisakufunire popumulako, kuti ukhale bwino? Nanga Bowazi wodziwana nafe, amene unakhala nao adzakazi ake? Taona, usiku uno apuntha barele popunthirapo. Usambe tsono, nudzole, nuvale zovala zako, nutsikire popunthirapo, koma usadziwike naye munthuyo, koma atatha kudya ndi kumwa ndiko. Ndipo kudzali, akagona, upenye apo ati agone, numuke, nuvundukule ku mapazi ake, nugone, ndi iyeyo adzakufotokozera zoyenera kuchita iwe. Ndipo ananena naye, Zonse muzinena ndidzachita. Pamenepo anatsikira popunthirapo, nachita zonse monga umo mpongozi wake adamuuza. Ndipo atatha Bowazi kudya ndi kumwa, nusekerera mtima wake, anakagona kuthungo kwa mulu wa tirigu; nadza iye kachetechete, navundukula ku mapazi ake, nagona. Ndipo kunali, pakati pa usiku munthuyo anadzidzimuka, natembenuka; ndipo taona pa mapazi ake pagona mkazi. Nati iye, Ndiwe yani? Nayankha iye, Ndine Rute mdzakazi wanu; mufunde mdzakazi wanu chofunda chanu, pakuti inu ndinu wondiombolera cholowa. Nati iye, Yehova akudalitse, mwana wanga. Chokoma chako wachichita potsiriza pano, chiposa chakuyamba chija, popeza sunatsata anyamata, angakhale osauka angakhale achuma. Ndipo tsopano, mwana wanga, usaope; ndidzakuchitira zonse unenazi; pakuti onse a pa mudzi wa anthu a mtundu wanga adziwa kuti iwe ndiwe mkazi waulemu. Tsopano ndipo, zoonadi, ine ndine wakukuombolera cholowa, koma pali wakukuombolera woposa ine. Gona usiku uno, ndipo kudzali m'mawa, akakuombolera, chabwino, akuombolere; koma ngati safuna kukuombolera, pali Yehova, ndidzakuombolera cholowa ndine; gona mpaka m'mawa. Nagona ku mapazi ake mpaka m'mawa; nalawira asanazindikirane anthu. Pakuti anati, Chisadziwike kuti mkaziyo anadza popunthirapo. Ndipo anati, Bwera nacho chofunda chako, nuchigwire; nachigwira iye; ndipo anayesa miyeso isanu ndi umodzi ya barele, namsenza; atatero analowa m'mudzi. Ndipo pamene anadza kwa mpongozi wake, iye anati, Wapeza bwanji, mwana wanga? Pamenepo anamfotokozera zonse anamchitira munthuyo. Natinso, Miyeso, iyi isanu ndi umodzi ya barele anandipatsa, pakuti anati, Usafike kwa mpongozi wako wopanda kanthu. Ndipo anati, Khala ulipo, mwana wanga, mpaka udziwa umo ukhalire mlandu; pakuti munthuyo sadzauleka mpaka atautha mlanduwo lero lino. Ndipo Bowazi anakwera kunka kuchipata, nakhala pansi pomwepo; ndipo taona, woombolera winayo adanena Bowazi analinkupita; nati iye, Iwe uje, patuka, khala pansi apa; napatuka iye, nakhala pansi. Ndipo anatenga amuna khumi a akulu a mudzi, nati, Mukhale pansi apa. Nakhala pansi iwo. Pamenepo anati kwa woombolerayo, Naomi anabwerayo ku dziko la Mowabu ati agulitse kadziko kaja kadali ka mbale wathu Elimeleki; ndipo ndati ndikuululira ichi, ndi kuti, Ugule aka pamaso pa nzika, ndi pamaso akulu a anthu a kwathu. Ukafuna kuombola ombola; koma ukapanda kuombola, undiuze, ndidziwe; pakuti palibe woombola koma iwe, ndi ine pambuyo pako. Pamenepo anati, Ndidzaombola. Nati Bowazi, Tsiku lomwelo ugula mundawo pa dzanja la Naomi, uugulanso kwa Rute, Mmowabu, mkazi wa wakufayo, kuukitsira dzina la wakufayo pa cholowa chake. Ndipo woombolera anati, Sindikhoza kuuombola kwa ine ndekha, ndingaononge cholowa changa; udzitengere wekha mphamvu yanga yakuombola; popeza sinditha kuombola. Koma kale m'Israele pakuombola ndi pakusinthana, kutsimikiza mlandu wonse, akatero: munthu avula nsapato yake, naipereka kwa mnansi wake; ndiwo matsimikizidwe m'Israele. Ndipo woombolayo anati kwa Bowazi, Udzigulire wekha kadzikoko. Navula nsapato yake. Nati Bowazi kwa akulu, ndi kwa anthu onse, Inu ndinu mboni lero lino kuti ndagula zonse za Elimeleki, ndi zonse za Kilioni, ndi Maloni, pa dzanja la Naomi. Ndiponso Rute Mmowabu, mkazi wa Maloni ndamgula akhale mkazi wanga kuukitsa dzina la wakufayo pa cholowa chake; kuti dzina la wakufayo lisaiwalike pakati pa abale ake, ndi pa chipata cha malo ake; inu ndinu mboni lero lino. Pamenepo anthu onse anali kuchipata, ndi akulu, anati, Tili mboni ife. Yehova achite kuti mkazi wakulowayo m'nyumba mwako ange Rakele ndi Leya, amene anamanga nyumba ya Israele, iwo awiri; nuchite iwe moyenera m'Efurata, numveke m'Betelehemu; ndi nyumba yako inge nyumba ya Perezi, amene Tamara anambalira Yuda, ndi mbeu imene Yehova adzakupatsa ya namwali uyu. Momwemo Bowazi anatenga Rute, nakhala iye mkazi wake; ndipo analowa kwa iye; nalola Yehova kuti aime, ndipo anabala mwana wamwamuna. Pamenepo akazi anati kwa Naomi, Adalitsike Yehova amene sanalole kuti akusowe woombolera lero; nilimveke dzina lake m'Israele. Nakhale uyu wakukubwezera moyo, ndi wodyetsa ukalamba wako; pakuti mpongozi wako amene akukonda, amene aposa ana amuna asanu ndi awiri kukuthandiza, anambala. Ndipo Naomi anamtenga mwanayo, namuika pachifuwa pake, nakhala mlezi wake. Ndi akazi anansi ake anamutcha dzina, ndi kuti, Kwa Naomi kwambadwira mwana; namutcha dzina lake Obedi; ndiye atate wa Yese atate wa Davide. Iyo ndiyo mibadwo ya Perezi; Perezi anabala Hezironi; ndi Hezironi anabala Ramu, ndi Ramu anabala Aminadabu; ndi Aminadabu anabala Nasoni, ndi Nasoni anabala Salimoni; ndi Salimoni anabala Bowazi, ndi Bowazi anabala Obedi; ndi Obedi anabala Yese, ndi Yese anabala Davide. Ndipo panali munthu wina wa ku Ramatayimu Zofimu, wa dziko la mapiri la Efuremu, dzina lake ndiye Elikana, mwana wake wa Yerohamu, mwana wa Elihu, mwana wa Tohu, mwana wa Zufu, Mwefuremu. Iyeyu anali nao akazi awiri; winayo dzina lake ndi Hana, mnzake dzina lake ndi Penina. Ndipo Penina anaona ana, koma Hana anali wouma. Ndipo munthuyo akakwera chaka ndi chaka kutuluka m'mudzi mwake kukalambira ndi kupereka nsembe kwa Mulungu wa makamu m'Silo. Ndipo pomwepo panali ana amuna awiri a Eli, ansembe a Yehova, ndiwo Hofeni ndi Finehasi. Ndipo pofika tsiku lakuti Elikana akapereka nsembe, iye anapatsa Penina mkazi wake, ndi ana ake onse, aamuna ndi aakazi, gawo lao; koma anapatsa Hana magawo awiri, chifukwa anakonda Hana, koma Yehova anatseka mimba yake. Ndipo womnyodolayo anamputa kwakukulu, kuti amuwawitse mtima, popeza Yehova anatseka mimba yake. Ndipo popeza munthuyo adatero chaka ndi chaka, popita mkaziyo kunyumba ya Yehova, mnzakeyo amamputa; chifukwa chake iye analira misozi, nakana kudya. Ndipo mwamuna wake Elikana anati kwa iye, Hana, umaliriranji? Ndipo umakaniranji kudya? Ndipo mtima wako uwawa ninji? Ine sindili wakuposa ana khumi kwa iwe kodi? Chomwecho Hana anauka atadya m'Silo, ndi kumwa. Ndipo Eli wansembeyo anakhala pa mpando wake pa mphuthu ya Kachisi wa Yehova. Ndipo mkaziyo anali ndi mtima wowawa, napemphera kwa Yehova, naliratu misozi; nalonjeza chowinda, nati, Yehova wa makamu, mukapenyera ndithu kusauka kwa mdzakazi wanu, ndi kukumbukira ine, ndi kusaiwala mdzakazi wanu, mukapatsa mdzakazi wanu mwana wamwamuna, ine ndidzampereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake, ndipo palibe lumo lidzapita pamutu pake. Ndipo panali, m'mene iye analikupempherabe pamaso pa Yehova, Eli anapenyerera pakamwa pake. Koma Hana ananena mu mtima; milomo yake inatukula, koma mau ake sanamveke; chifukwa chake Eli anamuyesa woledzera. Ndipo Eli anati kwa iye, Udzaleka liti kuledzera? Chotsa vinyo wako. Ndipo Hana anayankha, nati, Iai, mbuyanga. Ine ndili mkazi wa mtima wachisoni; sindinamwa vinyo kapena chakumwa chowawa, koma ndinatsanulira mtima wanga pamaso pa Yehova. Musamandiyesa mdzakazi wanu mkazi woipa; chifukwa kufikira lero ndinalankhula mwa kuchuluka kwa kudandaula kwanga ndi kuvutika kwanga. Pamenepo Eli anayankha nati, Pita ndi mtendere; ndipo Mulungu wa Israele akupatse chopempha chako unachipempha kwa Iye. Ndipo iye anati, Mumkomere mtima mdzakazi wanu. Chomwecho mkaziyo anamuka, nakadya, ndi nkhope yake siinakhalanso yachisoni. Ndipo iwo anauka mamawa, nalambira pamaso pa Yehova, nabwerera, nafikanso kwao ku Rama; ndipo Elikana anadziwa mkazi wake Hana, Yehova namkumbukira iye. Ndipo panali pamene nthawi yake inafika, Hana anaima, nabala mwana wamwamuna; namutcha dzina lake Samuele, nati, Chifukwa ndinampempha kwa Yehova, Ndipo munthuyo Elikana, ndi a pa banja lake onse, anakwera kukapereka kwa Yehova nsembe ya chaka ndi chaka, ndi ya chowinda chake. Koma Hana sadakwera, chifukwa kuti anati kwa mwamuna wake Sindidzakwerako kufikira mwanayo ataleka kuyamwa, pamenepo ndidzapita naye kuti aoneke pamaso pa Yehova, ndi kukhalako chikhalire. Ndipo Elikana mwamuna wake anati, Chita chimene chikukomera nukhale kufikira utamletsa kuyamwa; komatu Yehova akhazikitse mau ake. Chomwecho mkaziyo anakhala nayamwitsa mwana wake, kufikira anamletsa kuyamwa. Ndipo atamletsa kuyamwa anakwera naye, pamodzi ndi ng'ombe ya zaka zitatu, ndi efa wa ufa, ndi thumba la vinyo, nafika naye kunyumba ya Yehova ku Silo; koma mwanayo anali wamng'ono. Ndipo iwo anapha ng'ombe, nabwera naye mwanayo kwa Eli. Ndipo mkaziyo ananena, Mbuye wanga, pali moyo wanu, zoonadi ine ndine mkazi uja ndidaima pano ndi inu, ndi kupemphera kwa Yehova. Ndinampempha mwanayu; ndipo Yehova anandipatsa chopempha changa ndinachipempha kwa Iye; chifukwa chake inenso ndinampereka kwa Yehova; masiku onse a moyo wake aperekedwa kwa Yehova. Ndipo analambira Yehova pomwepo. Ndipo Hana anapemphera, nati, Mtima wanga umyuka mokondwera kwa Yehova, nyanga yanga yakwezeka mwa Yehova; pakamwa panga pakula kwa adani anga; popeza ndikondwera m'chipulumutso chanu. Palibe wina woyera ngati Yehova; palibe wina koma Inu nokha; palibenso thanthwe longa Mulungu wathu. Musalankhulenso modzikuza kwambiri motero; m'kamwa mwanu musatuluke zolulutsa; chifukwa Yehova ndi Mulungu wanzeru, ndipo Iye ayesa zochita anthu. Mauta a amphamvu anathyoka, koma okhumudwawo amangiridwa ndi mphamvu m'chuuno. Amene anakhuta anakasuma chakudya; koma anjalawo anachira; inde chumba chabala asanu ndi awiri; ndipo iye amene ali ndi ana ambiri achita liwondewonde. Yehova amapha, napatsa moyo; Iye amatsitsa kumanda, naukitsanso. Yehova asaukitsa, nalemeza; achepetsa, nakuzanso. Amuutsa waumphawi m'fumbi, nanyamula wosowa padzala, kukamkhalitsa kwa akalonga; ndi kuti akhale nacho cholowa cha chimpando cha ulemerero. Chifukwa nsanamira za dziko lapansi nza Yehova, ndipo Iye anakhazika dziko pa izo. Adzasunga mapazi a okondedwa ake, koma oipawo adzawakhalitsa chete mumdima; pakuti palibe munthu adzapambana ndi mphamvu. Otsutsana ndi Yehova adzaphwanyika; kumwamba Iye adzagunda pa iwo; Yehova adzaweruza malekezero a dziko. Ndipo adzapatsa mphamvu mfumu yake, nadzakweza nyanga ya wodzozedwa wake. Ndipo Elikana ananka kwao ku Rama, mwanayo natumikira Yehova pamaso pa Eli wansembeyo. Koma ana a Eli anali oipa; sanadziwe Yehova. Ndipo machitidwe a ansembe akuchitira anthu ndiwo, kuti pamene munthu aliyense akapereka nsembe, mnyamata wa wansembeyo akabwera, nyama ili chiwirire, ndi chovuulira cha ngowe cha mano atatu m'dzanja lake; nachipisa m'chimphuli, kapena mumkhate, kapena m'nkhali, kapena mumphika; yonse imene chovuuliracho chinaitulutsa, wansembeyo anaitenga ikhale yake. Ankatero ku Silo ndi Aisraele onse akufika kumeneko. Ngakhale asanayambe kupsereza mafuta, amadza mnyamata wa wansembe, namuuza wopereka nsembe, nati, Umpatse wansembeyo nyama yoti akaotche; pakuti safuna nyama yako yophika koma yaiwisi. Ndipo ngati munthu akanena naye, Koma adzatentha mafuta tsopano apa, atatha, utenge monga mtima wako ufuna; uyo akanena naye, Iai, koma undipatsire iyo tsopanoli, ukapanda kutero ndidzailanda. Ndipo zoipa za anyamatawo zinali zazikulu ndithu pamaso pa Yehova; pakuti anthu anaipidwa ndi nsembe ya Yehova. Koma Samuele anatumikira pamaso pa Yehova akali mwana, atamangira m'chuuno ndi efodi wabafuta. Ndiponso amake akamsokera mwinjiro waung'ono, nabwera nao kwa iye chaka ndi chaka, pakudza pamodzi ndi mwamuna wake kudzapereka nsembe ya pachaka. Ndipo Eli anadalitsa Elikana ndi mkazi wake, nati, Yehova akupatse mbeu ndi mkazi uyu m'malo mwa iye amene munampempha kwa Yehova. Ndipo iwowa anabwera kwao. Ndipo Yehova anakumbukira Hana, naima iye, nabala ana amuna atatu, ndi ana akazi awiri. Ndipo mwanayo Samuele anakula pamaso pa Yehova. Ndipo Eli anali wokalamba ndithu; namva zonse ana ake anachitira Aisraele onse, ndi kuti anagona ndi akazi akusonkhana pa khomo la chihema chokomanako. Ndipo iye ananena nao, Mumachitiranji chotere: popeza ndilinkumva za machitidwe anu oipa kwa anthu onsewa. Iai, ana anga, popeza mbiri imene ndilikuimva sili yabwino iai; mulikulakwitsa anthu a Yehova. Munthu akachimwira munthu mnzake oweruza adzaweruza mlandu wake; koma ngati munthu achimwira Yehova, adzampembedzera ndani? Koma ngakhale adatero, iwo aja anakhalabe osamvera mau a atate wao, chifukwa Yehova adati adzawaononga. Ndipo mwanayo Samuele anakulakula, ndipo Yehova ndi anthu omwe anamkomera mtima. Ndipo anafika kwa Eli munthu wa Mulungu, nanena naye, Atero Yehova, Kodi Ine ndinadziwulula kwa banja la kholo lako, muja anali m'Ejipito, m'nyumba ya Farao? Kodi sindinasankhula iye pakati pa mafuko onse a Israele, akhale wansembe wanga, kuti apereke nsembe pa guwa langa, nafukize zonunkhira, navale efodi pamaso panga? Kodi sindinapatsa banja la kholo lako zopereka zonse za kumoto za ana a Israele? Nanga umaponderezeranji nsembe yanga ndi chopereka changa, zimene ndinalamulira m'mokhalamo mwanga; ndipo uchitira ana ako ulemu koposa Ine, kudzinenepetsa inu nokha ndi zokometsetsa za zopereka zao zonse za Aisraele, anthu anga? Chifukwa chake Yehova Mulungu wa Israele akuti, Ndinaterodi kuti banja lako ndi banja la kholo lako lidzayenda pamaso panga nthawi zonse; koma tsopano Yehova ati, Chikhale kutali ndi Ine; popeza amene andilemekeza Ine, Inenso ndidzawalemekeza iwowa, ndipo akundipeputsa Ine, adzapeputsidwa. Ona, masiku alinkudza amene ndidzadula dzanja lako, ndi dzanja la nyumba ya kholo lako, kuti m'banja lako musakhalenso nkhalamba, Ndipo udzaona masautso a mokhalamo Mulungu, m'malo mwa zabwino zonse Iye akadachitira Israele. Banja lako lidzakhala opanda nkhalamba chikhalire. Ndipo munthu wako, amene ndidzamleka osamlikha pa guwa langa, adzatha maso ako, ndi kumvetsa mtima wako chisoni; ndipo obadwa onse a m'banja lako adzamwalira akali biriwiri. Ndipo ichi chimene chidzafikira ana ako awiri Hofeni ndi Finehasi, chidzakhala chizindikiro kwa iwo, tsiku limodzi adzafa iwo onse awiri. Ndipo ndidzadziukitsira wansembe wokhulupirika, amene adzachita monga chimene chili mumtima mwanga ndi m'chifuniro changa; ndipo ndidzammangira nyumba yokhazikika, ndipo iyeyu adzayenda pamaso pa wodzozedwa wanga masiku onse. Ndipo kudzali kuti yense wakusiyidwa wa m'banja lako adzabwera kwa iye nadzawerama ndi kupempha ndalama ndi chakudya, nadzati, Mundipatsetu ntchito ina ya wansembe, kuti ndikaona kakudya. Ndipo mwanayo Samuele anatumikira Yehova pamaso pa Eli. Ndipo masiku aja mau a Yehova anamveka kamodzikamodzi; masomphenya sanaonekeoneke. Ndipo kunali nthawi yomweyo Eli atagona m'malo mwake (maso ake anayamba chizirezire osatha kupenya bwino); ndi nyali ya Mulungu isanazime, Samuele nagona m'Kachisi wa Yehova, m'mene munali likasa la Mulungu. Pamenepo Yehova anaitana Samuele; ndipo iye anayankha kuti, Ndili pano. Ndipo anathamangira kwa Eli nati, Ndine, popeza mwandiitana ine. Ndipo iye anati, Sindinaitana, kagone. Napita iye, nagona. Ndipo Yehova anabwereza kumuitana, ndi kuti, Samuele. Ndipo Samuele anauka, napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Koma iye anayankha, Sindinaitana, mwana wanga; kagone. Koma Samuele sanadziwe Yehova, ndiponso mau a Yehova sanaululidwe kwa iye. Ndipo Yehova anabwereza kumuitana Samuele nthawi yachitatu. Ndipo iye anauka napita kwa Eli, nati, Ndine, pakuti mwandiitana ndithu. Ndipo Eli anazindikira kuti ndiye Yehova amene analikuitana mwanayo. Chifukwa chake Eli anati kwa Samuele, Pita, ukagone; ndipo akakuitananso, ukavomere, kuti, Nenani, Yehova, popeza mnyamata wanu akumva. Chomwecho Samuele anakagona m'malo mwake. Ndipo Yehova anabwera, naimapo, namuitana monga momwemo, Samuele, Samuele. Pompo Samuele anayankha, Nenani, popeza mnyamata wanu akumva. Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Taona, ndidzachita mwa Israele choliritsa mwini khutu kwa munthu yense wakuchimva. Tsiku lija ndidzamchitira Eli zonse ndinaneneratu za pa banja lake, kuchiyamba ndi kuchitsiriza. Popeza ndinamuuza kuti ndidzaweruza nyumba yake kosatha chifukwa cha zoipa anazidziwa, popeza ana ake anadzitengera temberero, koma iye sanawaletse. Chifukwa chake ndinalumbira kwa banja la Eli, kuti zoipa za banja la Elilo sizidzafafanizidwa ndi nsembe, kapena ndi zopereka, ku nthawi zonse. Ndipo Samuele anagona kufikira m'mawa, natsegula zitseko za nyumba ya Yehova. Ndipo Samuele anaopa kudziwitsa Eli masomphenyawo. Pamenepo Eli anaitana Samuele, nati, Mwana wanga, Samuele. Nati iye, Ndine. Ndipo anati, Anakuuza chinthu chanji? Usandibisire ine. Mulungu akulange, ndi kuonjezapo, ngati undibisira chimodzi cha zonse zija adanena nawe. Ndipo Samuele anamuuza zonse, sanambisire kanthu. Ndipo iye anati, Ndiye Yehova; achite chomkomera pamaso pake. Ndipo Samuele anakula, Yehova nakhala naye, osalola kuti mau ake amodzi apite pachabe. Ndipo Aisraele onse, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba anazindikira kuti Samuele anakhazikika akhale mneneri wa Yehova. Ndipo Yehova anaonekanso m'Silo, pakuti Yehova anadziwulula kwa Samuele ku Silo, mwa mau a Yehova. Ndipo mau a Samuele anafikira kwa Aisraele onse. Ndipo Aisraele anatuluka kukaponyana nkhondo ndi Afilisti, namanga zithando zao ku Ebenezeri; Afilistiwo namanga m'Afeki. Ndipo Afilistiwo anandandalitsa nkhondo yao pa Aisraele; ndipo pokomana nkhondo Aisraele anakanthidwa ndi Afilisti. Ndipo anapha kuthengoko anthu zikwi zinai a khamu lao. Ndipo pamene anthu anafika ku zithandozo, akulu a Israele anati, Yehova anatikanthiranji lero pamaso pa Afilisti? Tikadzitengere likasa la chipangano la Yehova ku Silo, kuti likabwera pakati pa ife, lidzatipulumutsa m'dzanja la adani athu. Chifukwa chake anatumiza ku Silo kuti akatenge kumeneko likasalo la chipangano la Yehova wa makamu, wokhala pakati pa akerubi; ndipo ana awiriwo a Eli, Hofeni ndi Finehasi anali komweko ndi likasa la chipangano la Yehova. Pakufika likasalo la chipangano la Yehova kuzithando, Aisraele onse anafuula ndi mau okweza, kotero kuti dziko linachita chivomezi. Ndipo Afilistiwo pakumva kubuma pa kufuula kwao, anati, Phokoso ili la kufuula kwakukulu ku zithando za Aisraele n'lachani? Ndipo anamva kuti likasa la Yehova lidafika ku zithandozo. Ndipo Afilisti anaopa, pakuti anati, Mulungu wafika kuzithando. Ndipo iwo anati, Tsoka kwa ife! Popeza kale lonse panalibe chinthu chotere. Tsoka kwa ife! Adzatilanditsa ndani m'manja a milungu yamphamvu imeneyi? Milungu ija inakantha Aejipito ndi masautso onse m'chipululu ndi yomweyi. Limbikani, ndipo muchite chamuna, Afilisti inu, kuti mungakhale akapolo a Ahebri, monga iwowa anali akapolo anu. Chitani chamuna nimuponyane nao. Ndipo Afilisti anaponyana nao, nakantha Aisraele; iwowa nathawira, munthu yense ku hema wake; ndipo kunali kuwapha kwakukulu; popeza anafako Aisraele zikwi makumi atatu a oyenda pansi. Ndipo likasa la Mulungu linalandidwa, ndi ana awiri a Eli, Hofeni ndi Finehasi, anaphedwa. Ndipo munthu wa fuko la Benjamini anathamanga kuchokera ku khamu la ankhondo, nafika ku Silo tsiku lomwelo, ndi zovala zake zong'ambika, ndi dothi pamutu pake. Pakufika iye, onani, Eli analikukhala pampando m'mbali mwa njira, alikuyang'anira, popeza mtima wake unanthunthumira chifukwa cha likasa la Mulungu. Pamene munthu uja anafika m'mudzimo, nanena izi, a m'mudzi monse analira. Ndipo Eli, pakumva kubuma kwa kulira kwao, anati, Alikupokoseranji? Ndipo munthuyo anafulumira, nadza nauza Eli. Koma Eli anali ndi zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zitatu; ndipo maso ake anangokhala tong'o osapenya. Ndipo munthuyo anati kwa Eli, Ine ndine amene ndachokera ku khamu la ankhondo, ndipo ndathawa lero ku khamu la ankhondo. Ndipo iye anati, Nkhondoyo idatani, mwana wanga? Ndipo wakubwera ndi mauyo anayankha, nati, Israele anathawa pamaso pa Afilisti, ndiponso kunali kuwapha kwakukulu kwa anthu, ndi ana anu awiri omwe Hofeni ndi Finehasi afa, ndipo likasa la Mulungu lalandidwa. Ndipo kunali, pakunena za likasa la Mulungu, iye anagwa chambuyo pa mpando wake pambali pa chipata, ndi khosi lake linathyoka, nafa iye; popeza anali wokalamba ndi wamkulu thupi. Ndipo adaweruza anthu a Israele zaka makumi anai. Ndipo mpongozi wake, mkazi wa Finehasi, anali ndi mimba, pafupi pa nthawi yake yakuona mwana; ndipo pakumva iye mau akuti likasa la Mulungu linalandidwa, ndi kuti mpongozi wake, ndi mwamuna wake anafa, iyeyu anawerama, nabala mwana; popeza kuchira kwake kwamdzera. Ndipo pamene adati amwalire, anthu akazi akukhala naye ananena, Usaope, popeza waona mwana wamwamuna. Koma iye sanayankhe, kapena kusamalira. Ndipo iye anamutcha dzina la mwanayo Ikabodi, nati, Ulemerero wachoka kwa Israele; chifukwa likasa la Mulungu linalandidwa, ndi chifukwa cha mpongozi wake ndi mwamuna wake. Ndipo iye anati, Ulemerero wachoka kwa Israele; chifukwa likasa la Mulungu lalandidwa. Ndipo Afilisti anatenga likasa la Mulungu, nachoka nalo ku Ebenezeri, napita ku Asidodi. Ndipo Afilistiwo anatenga likasa la Mulungu, nafika nalo kunyumba ya Dagoni, naliika pafupi ndi Dagoni. Ndipo pakuuka a ku Asidodi mamawa taonani Dagoni adagwa pansi, nagona chafufumimba patsogolo pa likasa la Yehova. Ndipo iwo anatenga Dagoni namuimikanso m'malo mwake. Ndipo m'mawa mwake polawirira, taonani, Dagoni adagwa pansi, nagona chafufumimba patsogolo pa likasa la Yehova; ndipo mutu wake ndi zikhato zonse ziwiri za manja ake zinagona zoduka pachiundo; Dagoni anatsala thupi lokha. Chifukwa chake angakhale ansembe, angakhale ena akulowa m'nyumba ya Dagoni, palibe woponda pa chiundo cha Dagoni ku Asidodi, kufikira lero lino. Koma Yehova anavuta iwo a ku Asidodi ndi dzanja lake, nawaononga, nawazunza ndi mafundo, m'Asidodi ndi m'milaga yake. Ndipo pamene anthu a ku Asidodi anaona kuti nchomwecho, anati iwowa, Likasa la Mulungu wa Israele lisakhalitse ndi ife; popeza dzanja lake litiwawira ife, ndi Dagoni mulungu wathu. Chifukwa chake anatumiza mithenga, nasonkhanitsa mafumu onse a Afilisti, nati Tichite nalo chiyani likasa la Mulungu wa Israele? Ndipo anati, Anyamule likasa la Mulungu kunka nalo ku Gati. Ndipo ananyamula likasalo la Mulungu wa Israele, napita nalo kumeneko. Ndipo kunali atafika nalo, dzanja la Yehova linatsutsa mudziwo ndi kusautsa kwakukulu; ndipo anazunza anthu a mudziwo, akulu ndi ang'ono; ndi mafundo anawabuka. Chifukwa chake anatumiza likasa la Mulungu ku Ekeroni. Ndipo kunali pofika likasalo ku Ekeroni, a ku Ekeroni anafuula nati, Anadzatitulira likasa la Mulungu wa Israele, kutipha ife ndi ana athu. Chifukwa chake anatumiza, nasonkhanitsa mafumu onse a Afilisti, ndipo iwowa anati, Chotsani likasa la Mulungu wa Israele, lipitenso kumalo kwake, kuti lingationonge ife, ndi anthu athu; pakuti kunali kusautsa koopsa m'mudzi monse; dzanja la Mulungu linavutadi pamenepo. Ndipo amene anapanda kufa anagwidwa ndi mafundowo; ndi kulira kwa mudziwo kunakwera kumwamba. Ndipo likasa la Yehova linakhala ku dziko la Afilisti miyezi isanu ndi iwiri. Ndipo Afilistiwo anaitana ansembe ndi oombeza, nati, Tichitenji ndi likasa la Yehova? Mutidziwitse chimene tilitumize nacho kumalo kwake. Ndipo iwo anati, Ngati mulitumiza kwina likasa la Mulungu wa Israele, musalitumize lopanda kanthu; koma makamaka mulibweze ndi nsembe yopalamula, mukatero mudzachiritsidwa, ndi kudziwa chifukwa chake dzanja lake lili pa inu losachoka. Ndipo iwo aja anati, Tidzambwezera nsembe yopalamula yanji? Ndipo iwo anati, Mafundo asanu agolide, ndi mbewa zisanu zagolide, monga mwa chiwerengo cha mafumu a Afilisti; popeza kusauka kumodzi kunali pa inu nonse, ndi pa mafumu anu. Chifukwa chake muzipanga zifanizo za mafundo anu, ndi zifanizo za mbewa zanu zimene ziipitsa dziko; ndipo muchitire ulemu Mulungu wa Israele; kuti kapena adzaleza dzanja lake pa inu, ndi pa milungu yanu, ndi pa dziko lanu. Mulikuumitsiranji mitima yanu, monga Aejipito ndi Farao anaumitsa mitima yao? Kodi iwo sanalole anthuwo amuke, Iye atachita kodabwitsa pakati pao, ndipo anamuka? Chifukwa chake tsono, tengani, nimukonze galeta latsopano, ndi ng'ombe ziwiri zamkaka, zosalawa goli chikhalire, ndipo mumange ng'ombezo pagaleta, muzichotsere ana ao kunka nao kwanu; ndipo mutenge likasa la Yehova, nimuliike pagaletapo; nimuike zokometsera zagolide, zimene muzipereka kwa Iye ngati nsembe yopalamula, m'bokosi pambali pake; nimulitumize lichoke. Ndipo muyang'anire, ngati likwera pa njira ya malire akeake ku Betesemesi, Iye anatichitira choipa ichi chachikulu; koma likapanda kutero, tidzadziwapo kuti dzanja limene linatikantha, silili lake; langotigwera tsokali. Ndipo anthuwo anatero; natenga ng'ombe ziwiri zamkaka, nazimanga pagaleta, natsekera anao kwao; naika likasa la Yehova pagaletapo, ndi bokosi m'mene munali mbewa zagolide ndi zifanizo za mafundo ao. Ndipo ng'ombezo zinatsata njira yolunjika ku Betesemesi, niziyenda mumseu, zilikulira poyenda; sizinapatukira ku dzanja lamanja, kapena kulamanzere; ndipo mafumu a Afilisti anazitsatira kufikira ku malire a Betesemesi. Ndipo a ku Betesemesi analikumweta tirigu wao m'chigwamo; natukula maso ao, naona likasalo, nakondwera pakuliona. Ndipo galetalo linafika m'munda wa Yoswa wa ku Betesemesi, ndi kuima momwemo, pa mwala waukulu; ndipo anawaza matabwa a galetalo, nazipereka ng'ombezo nsembe yopsereza kwa Yehova. Ndipo Alevi anatsitsa likasa la Yehova, ndi bokosi linali nalo, m'mene munali zokometsera zagolide, naziika pa mwala waukuluwo; ndipo anthu a ku Betesemesi anapereka nsembe zopsereza, naphera nsembe kwa Yehova tsiku lomwelo. Ndipo pamene mafumu asanu a Afilisti anaonerako, anabwerera kunka ku Ekeroni tsiku lomwelo. Ndipo amenewa ndiwo mafundo agolide amene Afilisti anabwezera kwa Yehova akhale nsembe yopalamula, kwa Asidodi limodzi, kwa Gaza limodzi, kwa Asikeloni limodzi, kwa Gati limodzi, kwa Ekeroni limodzi; ndiponso mbewa zagolide, monga chiwerengo cha midzi yonse ya mafumu asanu a Afilisti, midzi ya malinga, ndi midzi ya kumilaga; kufikira ku mwala waukulu, adaikapo likasa la Yehova; mwalawo ulipobe kufikira lero m'munda wa Yoswa wa ku Betesemesi. Ndipo Mulungu anakantha anthu a ku Betesemesi, chifukwa anasuzumira m'likasa la Yehova, anakantha anthu zikwi makumi asanu; ndipo anthu analira maliro, chifukwa Yehova anawakantha anthuwo ndi makanthidwe akulu. Ndipo a ku Betesemesi anati, Akhoza ndani kuima pamaso pa Yehova, Mulungu Woyera uyu? Ndipo adzakwera kwa yani pakutichokera ife? Ndipo anatumiza mithenga kwa anthu a ku Kiriyati-Yearimu, nati, Afilisti anabwera nalo likasa la Yehova, mutsike; ndi kukwera nalo kwanu. Ndipo anthu a ku Kiriyati-Yearimu anabwera, natenga likasa la Yehova, nafika nalo m'nyumba ya Abinadabu paphiri; napatula mwana wake wamwamuna Eleazara kuti asunge likasa la Yehova. Ndipo kunali, kuti likasalo linakhala nthawi yaikulu m'Kiriyati-Yearimu; popeza linakhalako zaka makumi awiri; ndipo banja lonse la Israele linalirira Yehova. Ndipo Samuele analankhula ndi banja lonse la Israele nati, Ngati mukuti mubwerere kunka kwa Yehova ndi mitima yanu yonse, chotsani pakati pa inu milungu yachilendo, ndi Asitaroti, nimukonzere Yehova mitima yanu, ndi kumtumikira Iye yekha; mukatero, Iye adzakupulumutsani m'manja a Afilisti. Pomwepo ana a Israele anachotsa Abaala ndi Asitaroti, natumikira Yehova yekha. Ndipo Samuele anati, Musonkhanitse Aisraele onse ku Mizipa, ndipo ine ndidzakupemphererani kwa Yehova. Ndipo anaunjikana ku Mizipa, natunga madzi, nawatsanula pamaso pa Yehova, nasala chakudya tsiku lija, nati, Tinachimwira Yehova. Ndipo Samuele anaweruza ana a Israele m'Mizipa. Ndipo pamene Afilisti anamva kuti Aisraele anasonkhana pamodzi ku Mizipa, mafumu a Afilisti anakwera kukayambana ndi Aisraele. Ndipo Aisraele pakumva ichi, anachita mantha ndi Afilistiwo. Ndipo ana a Israele anati kwa Samuele, Musaleke kutipempherera kwa Yehova Mulungu wathu, kuti Iye atipulumutse m'manja a Afilistiwo. Ndipo Samuele anatenga mwanawankhosa woyamwa, nampereka wathunthu kwa Yehova, nsembe yopsereza; ndipo Samuele anapempherera Israele kwa Yehova; ndipo Yehova anamvomereza. Ndipo pamene Samuele analikupereka nsembe yopserezayo, Afilisti anayandikira kuti aponyane ndi Aisraele; koma tsiku lomwe lija Yehova anagunda ndi kugunda kwakukulu pa Afilistiwo, nawapolonganitsa. Ndipo anakanthidwa pamaso pa Aisraele. Ndipo Aisraele anatuluka ku Mizipa, nathamangira Afilisti, nawakantha mpaka anafika pansi pa Betekara. Pamenepo Samuele anatenga mwala nauimika pakati pa Mizipa ndi Sene, nautcha dzina lake Ebenezeri, nati, Kufikira pano Yehova anatithandiza. Chomwecho anagonjetsa Afilisti, ndipo iwo sanatumphenso malire a Israele ndipo dzanja la Yehova linasautsa Afilisti masiku onse a Samuele. Ndipo midzi ya Israele imene Afilisti adailanda kale inabwezedwa kwa Aisraele, kuyambira ku Ekeroni kufikira ku Gati; ndi Aisraele analanditsa milaga yao m'manja a Afilisti. Ndipo pakati pa Aisraele ndi Aamori panali mtendere; ndipo Samuele anaweruza Israele masiku onse a moyo wake. Ndipo anayenda chozungulira chaka ndi chaka ku Betele, ndi ku Giligala, ndi ku Mizipa; naweruza Israele m'malo onse amenewa. Ndipo anabwera ku Rama, pakuti nyumba yake inali kumeneko; ndipo pamenepo anaweruza Israele; namangapo guwa la nsembe la Yehova. Ndipo kunali, pamene Samuele anakalamba, anaika ana ake amuna akhale oweruza a Israele. Dzina la mwana wake woyamba ndiye Yowele, ndi dzina la wachiwiri ndiye Abiya; ndiwo oweruza a ku Beereseba. Ndipo ana ake sanatsanze makhalidwe ake, koma anapatukira ku chisiriro, nalandira chokometsera mlandu, naipitsa kuweruza. Pamenepo akulu onse a Israele anasonkhana, nadza kwa Samuele ku Rama; nanena naye, Taonani, mwakalamba, ndipo ana anu satsanza makhalidwe anu; tsono, mutilongere mfumu kuti ikatiweruze, monga umo muchitidwa m'mitundu yonse ya anthu. Koma chimenechi sichinakondweretsa Samuele, pamene iwo anati, Tipatseni mfumu kuti itiweruze. Ndipo Samuele anapemphera kwa Yehova. Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Umvere mau onse anthuwo alikulankhula nawe; popeza sindiwe anakukana, koma ndine anandikana, kuti ndisakhale mfumu yao. Monga ntchito zao zonse anazichita kuyambira tsiku lija ndinawatulutsa ku Ejipito, kufikira lero lino kuti anandisiya Ine, natumikira milungu ina, momwemo alikutero ndi iwenso. Chifukwa chake tsono umvere mau ao; koma uwachenjeze kolimba, ndi kuwadziwitsa makhalidwe ake a mfumu imene idzawaweruza. Ndipo Samuele anauza anthu akumpempha iye mfumu mau onse a Yehova. Nati, Awa ndi makhalidwe a mfumu imene idzaweruza inu; idzatenga ana anu amuna, akhale akusunga magaleta, ndi akavalo ake; ndipo adzathamanga ndi kutsogolera magaleta ake; idzawaika akhale otsogolera chikwi, ndi otsogolera makumi asanu; ndipo idzaika ena kulima minda yake, ndi kutema dzinthu zake, ndi kumpangira zipangizo za nkhondo, ndi zipangizo za magaleta. Ndipo idzatenga ana anu akazi apange zonunkhira, naphikire, naumbe mikate. Ndipo idzalanda minda yanu, ndi minda ya mphesa yanu, ndi minda ya azitona, inde minda yoposayo, nidzaipatsa anyamata ake. Ndipo idzatenga limodzi la magawo khumi la mbeu zanu, ndi la minda yanu yamphesa, nidzalipatsa akapitao ake, ndi anyamata ake. Ndipo idzatenga akapolo anu, ndi adzakazi anu, ndi anyamata anu okongola koposa, ndi abulu anu, nidzawagwiritsa ntchito yake. Idzatenga limodzi la magawo khumi la zoweta zanu; ndipo inu mudzakhala akapolo ake. Ndipo tsiku lija mudzafuula chifukwa cha mfumu yanu munadzisankhira nokha; koma Yehova sadzayankha inu tsiku lijalo. Koma anthu anakana kumvera mau a Samuele; nati, Iai, koma tifuna kukhala nayo mfumu yathu; kuti ifenso tikafanane nao anthu a mitundu yonse; kuti mfumu yathuyo ikatiweruzire, ndi kutuluka kutitsogolera, ndi kuponya nafe nkhondo zathu. Ndipo Samuele anamva mau onse a anthuwo, nawafotokozanso m'makutu a Yehova. Ndipo Yehova anati kwa Samuele, Umvere mau ao, nuwalongere mfumu. Ndipo Samuele anati kwa amuna a Israele, Mupite, munthu yense kumudzi wake. Ndipo panali munthu Mbenjamini, dzina lake ndiye Kisi, mwana wa Abiyele, mwana wa Zerori, mwana wa Bekorati, mwana wa Afiya, mwana wa Mbenjamini, ndiye ngwazi. Iye anali ndi mwana wamwamuna dzina lake Saulo, mnyamata wokongola; pakati pa anthu onse a Israele panalibe wina wokongola ngati iye; anali wamtali, anthu onse ena anamlekeza m'chifuwa. Ndipo abulu a Kisi, atate wa Saulo, analowerera. Ndipo Kisi anati kwa Saulo mwana wake, Utenge mnyamata mmodzi, nunyamuke, kukafuna abuluwo. Ndipo anapyola dziko lamapiri la Efuremu, napyola dziko la Salisa, koma sanawapeze; pamenepo anapyolanso dziko la Salimu, koma panalibe pamenepo, napyola dziko la Abenjamini, osawapeza. Pamene anafika ku dziko la Zufu, Saulo anamuuza mnyamata amene anali naye, kuti, Tiye tibwerere; kuti atate wanga angaleke kusamalira abuluwo, ndi kutenga nkhawa chifukwa cha ife. Koma ananena naye, Onatu, m'mudzi muno muli munthu wa Mulungu, ndiye munthu anthu amchitira ulemu; zonse azinena zichitika ndithu; tiyeni tipite komweko, kapena adzakhoza kutidziwitsa zimene tili kuyendera. Ndipo Saulo ananena ndi mnyamata wake, Koma taona, tikapitako timtengere chiyani munthuyo? Popeza mkate udatha m'zotengera zathu, ndiponso tilibe mphatso yakumtengera munthu wa Mulungu, tili nacho chiyani? Ndipo mnyamatayo anayankhanso kwa Saulo nati, Onani m'dzanja langa muli limodzi la magawo anai a sekeli wa siliva; ndidzampatsa munthu wa Mulungu limeneli kuti atiuze njira yathu. Kale m'Israele, munthu akati afunse kwa Mulungu, ankatero kuti, Tiyeni tipite kwa mlauliyo; popeza iye wotchedwa mneneri makono ano, anatchedwa mlauli kale. Pamenepo Saulo anati kwa mnyamata wake, Wanena bwino; tiye tipite. Chomwecho iwowa anapita kumudzi kumene kunali munthu wa Mulunguyo. Pakukwera kumudziko anapeza anthu akazi alikutuluka kuti akatunge madzi, nanena nao, Mlauliyo alipo kodi? Ndipo anawayankha nati, Alipo; onani ali m'tsogolo mwanu; fulumirani pakuti wabwera lero kumudzi kuno; popeza lero anthu akuti aphere nsembe pamsanje; mutafika m'mudzi, pomwepo mudzampeza, asanakwere kumsanje kukadya; pakuti anthu sadzadya, koma iye atafika ndipo; pakuti iye amadalitsa nsembeyo; ndipo atatero oitanidwawo amadya. Chifukwa chake kwerani; popeza nthawi yino mudzampeza. Ndipo iwowa anakwera kumudzi; ndipo m'mene analowa m'mudzimo, onani, Samuele anatulukira pali iwo, kuti akakwere kumsanje. Ndipo Yehova anaululiratu m'khutu la Samuele dzulo lake la tsiku limene Saulo anabwera, kuti, Mawa, monga dzuwa lino, ndidzakutumizira munthu wochokera ku dziko la Benjamini, udzamdzoza iye akhale mtsogoleri wa anthu anga Israele, kuti akawapulumutse anthu anga m'manja a Afilisti; pakuti Ine ndinapenya pa anthu anga, popeza kulira kwao kunandifika Ine. Ndipo pamene Samuele anaona Saulo, Yehova anati kwa iye, Ona munthu amene ndinakuuza za iye! Ameneyu adzaweruza anthu anga. Pomwepo Saulo anayandikira kwa Samuele pakati pa chipata, nati, Mundidziwitse nyumba ya mlauliyo ili kuti. Ndipo Samuele anayankha Saulo nati, Ine ndine mlauliyo. Kwera, batsogola kumsanje, pakuti mudzadya ndi ine lero; ndipo m'mawa ndidzakulola upite, ndi kukudziwitsa zonse zili mumtima mwako. Za abulu ako atatayika adapita masiku atatu, usalingalirenso iwowa; pakuti anapezedwa. Ndipo chifuniro chonse cha Israele chili kwa yani? Si kwa iwe ndi banja lonse la atate wako? Ndipo Saulo anayankha nati, Sindili Mbenjamini kodi wa fuko laling'ono mwa Israele? Ndiponso banja lathu nlochepa pakati pa mabanja onse a fuko la Benjamini? Potero mulankhula bwanji mau otere ndi ine? Ndipo Samuele anatenga Saulo ndi mnyamata wake, napita nao ku chipinda cha alendo, nawakhalitsa pa malo a ulemu pakati pa oitanidwa onse; ndiwo anthu monga makumi atatu. Ndipo Samuele ananena ndi wophika, Tenga nyama ndinakupatsa, ndi kuti, Ibakhala ndi iwe. Ndipo wophikayo ananyamula mwendo ndi mnofu wake, nauika pamaso pa Saulo. Ndipo Samuele anati, Onani chimene tinakuikirani? Muchiike pamaso panu, nudye; pakuti ichi anakuikirani kufikira nthawi yonenedwa, popeza ndinati, Ndinaitana anthuwo. Chomwecho Saulo anadya ndi Samuele tsiku lija. Ndipo pamene anatsika kumsanje kulowanso kumudzi, iye anakamba ndi Saulo pamwamba pa nyumba yake. Ndipo anauka mamawa; ndipo kutacha, Samuele anaitana Saulo ali pamwamba pa nyumba, nati, Ukani kuti ndikuloleni mumuke. Ndipo Saulo anauka, natuluka onse awiri, iye ndi Samuele, kunka kunja. Ndipo pamene analikutsika polekeza mudzi, Samuele ananena ndi Saulo, Uzani mnyamatayo abatsogola; napita iyeyo. Koma inu muime pano, kuti ndikumvetseni mau a Mulungu. Pamenepo Samuele anatenga nsupa ya mafuta, nawatsanulira pamutu pake, nampsompsona iye, nati, Sanakudzozeni ndi Yehova kodi, Mukhale mfumu ya pa cholowa chake? M'mene talekana lero, mudzakomana ndi anthu awiri pa manda a Rakele, pa malire a Benjamini ku Zeliza; iwo ndiwo adzanena nanu, Abulu aja munakafuna, anapezedwa; ndipo onani, atate wanu analeka kulingalira abuluwo, koma alikulingalira za inu, ndi kuti, Ndidzachita chiyani, chifukwa cha mwana wanga? Mukapitirira pamenepo tsono ndi kufika ku mtengo wathundu wa ku Tabori, kumeneko adzakomana nanu anthu atatu akukwera kwa Mulungu ku Betele, wina wonyamula anaambuzi atatu, wina mikate itatu, wina thumba la vinyo. Iwowa adzakupatsani moni, ndi kukupatsani mikate iwiri; imeneyi mudzailandira m'manja mwao. Ndipo m'tsogolo mwake mudzafika kuphiri la Mulungu, kumene kuli kaboma ka Afilisti; ndipo kudzali kuti pakufika inu kumudziko mudzakomana ndi gulu la aneneri, alikutsika kumsanje ndi chisakasa, ndi lingaka, ndi chitoliro, ndi zeze, pamaso pao; iwo adzanenera; ndipo Mzimu wa Yehova udzagwera inu kolimba, nanunso mudzanenera pamodzi nao, nimudzasandulika munthu wina. Ndipo zitakufikirani zizindikiro izi mudzachita monga mudzaona pochita, pakuti Mulungu ali nanu. Ndipo mudzatsika patsogolo pa ine kunka ku Giligala; ndipo, taonani, ndidzatsikira kwa inu kukapereka zopsereza, ndi kuphera nsembe zamtendere. Mutsotsepo masiku asanu ndi awiri kufikira ndikatsikira kwa inu ndi kukudziwitsani chimene mudzachita. Ndipo kunali, pamene iye anapotoloka kuti alekane ndi Samuele, Mulungu anampatsa mtima wina watsopano; ndipo zizindikiro zija zonse zinachitika tsiku lija. Ndipo pamene anafika ku Gibea, onani, gulu la aneneri linakomana naye; ndi Mzimu wa Mulungu unamgwera mwamphamvu, iye nanenera pakati pao. Ndipo kunali, kuti onse amene anamdziwiratu kale, pakuona ichi chakuti, onani, iye ananenera pamodzi ndi aneneri, anati wina ndi mnzake, Ichi nchiyani chinamgwera mwana wa Kisi? Kodi Saulonso ali mwa aneneri? Ndipo munthu wina wa komweko anayankha nati, Ndipo atate wao ndiye yani? Chifukwa chake mauwa anakhala ngati mwambi, Kodi Saulonso ali mwa aneneri? Ndipo pamene adatha kunenera anafika kumsanjeko. Ndipo mbale wa atate wake wa Saulo ananena kwa iye ndi mnyamata wake, Munanka kuti? Ndipo iye anati, Kukafuna abuluwo; ndipo pakuona kuti sitinawapeza, tinadza kwa Samuele. Ndipo mbale wa atate wa Saulo anati, Undiuze chimene Samuele analankhula nawe. Ndipo Saulo anati kwa mbale wa atate wake, Anatiuza momveka kuti abuluwo anapezedwa kale. Koma sanamdziwitse mau aja Samuele ananena za ufumuwo. Ndipo Samuele anaitana anthu onse asonkhane kwa Yehova ku Mizipa; nanena ndi ana a Israele, Atero Yehova, Mulungu wa Israele kuti, Ine ndinatulutsa Israele m'Ejipito, ndipo ndinakupulumutsani m'manja a Aejipito, ndi m'manja a maufumu onse anakusautsani; koma lero inu mwakana Mulungu wanu amene anakupulumutsani yekha m'matsoka anu onse, ndi m'masautso anu; ndipo munanena naye, Koma mutipatse mfumu. Chifukwa chake tsono mudzionetse pamaso pa Yehova mafukomafuko, ndi magulumagulu. Chomwecho Samuele anayandikizitsa mafuko onse a Israele, ndipo fuko la Benjamini linasankhidwa. Nayandikizitsa fuko la Benjamini, banja ndi banja, ndipo banja la Amatiri linasankhidwa; nasankhidwa Saulo mwana wa Kisi. Koma pamene anamfuna, anapeza palibe. Chifukwa chake anaonjeza kufunsa Yehova, Watsala wina kodi woyenera kubwera kuno? Ndipo Yehova anati, Onani, alikubisala pakati pa akatundu. Ndipo anathamanga, namtenga komweko; ndipo iye pamene anaima pakati pa anthuwo, anali wamtali koposa anthu onse anamlekeza m'chifukwa. Ndipo Samuele ananena ndi anthu onse, Mumuona kodi iye amene Yehova anamsankha, kuti palibe wina wakufanana naye pakati pa anthu onse? Ndipo anthu onse anafuula, kuti, Akhale ndi moyo mfumuyo. Pamenepo Samuele anafotokozera anthu machitidwe a ufumu, nawalembera m'buku, nalisunga pamaso pa Yehova. Ndipo Samuele anauza anthu onse amuke, yense kunyumba yake. Ndi Saulo yemwe anamuka kunyumba yake ku Gibea; ndipo am'khamu anatsagana naye iwo amene Mulungu adakhudza mitima yao. Koma oipa ena anati, Uyu adzatipulumutsa bwanji? Ndipo anampeputsa, osakampatsa mtulo. Koma iye anakhala chete. Pamenepo Nahasi Mwamoni anakwera, namanga Yabesi-Giliyadi zithando; ndipo anthu onse a ku Yabesi anati kwa Nahasi, Mupangane chipangano ndi ife, ndipo tidzakutumikirani inu. Ndipo Nahasi Mwamoni ananena nao, Ndidzapangana nanu, ngati mulola kuti maso a ku dzanja lamanja anu onse akolowoledwe; potero ndidzanyazitsa Aisraele onse. Ndipo akulu a ku Yabesi ananena naye, Mutipatse masiku asanu ndi awiri, kuti titumize mithenga m'malire onse a Israele; ndipo pakapanda kuoneka wotipulumutsa ife, tidzatulukira kwa inu. Tsono mithengayo inafika ku Gibea kwa Saulo, nalankhula mau amenewa m'makutu a anthu; ndipo anthu onse anakweza mau, nalira misozi. Ndipo, onani, Saulo anachokera kumunda alikutsata ng'ombe; nati Saulo, Choliritsa anthu misozi nchiyani? Ndipo anamuuza mau a anthu a ku Yabesi. Ndipo mzimu wa Mulungu unamgwera Saulo mwamphamvu, pamene anamva mau awa, ndi mkwiyo wake unayaka kwambiri. Natenga ng'ombe ziwiri nazidula nthulinthuli, nazitumiza m'malire monse mwa Israele, ndi dzanja la mithenga, nati, Amene sakudza pambuyo pa Saulo ndi pa Samuele, adzatero nazo ng'ombe zake. Ndipo kuopsa kwa Yehova kunawagwera anthu, natuluka ngati munthu mmodzi. Ndipo anawawerenga ku Bezeki; ndipo ana a Israele anali zikwi mazana atatu, ndi anthu a Yuda ndiwo zikwi makumi atatu. Ndipo anati kwa mithenga inadzayi, Muzitero kwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi, Mawa litatentha dzuwa, mudzaona chipulumutso. Ndipo mithenga inadza niuza a ku Yabesi; nakondwera iwowa. Chifukwa chake anthu a ku Yabesi anati, Mawa tidzatulukira kwa inu, ndipo mudzatichitira chokomera inu. Ndipo m'mawa mwake Saulo anagawa anthu magulu atatu; ndipo iwowa anafika pakati pa zithandozo m'ulonda wa mamawa, nakantha Aamoni kufikira kutentha kwa dzuwa. Ndipo otsalawo anabalalika, osatsala pamodzi ngakhale awiri. Ndipo anthu anati kwa Samuele, Ndani iye amene anati, Kodi Saulo adzatiweruza ife? Tengani anthuwo kuti tiwaphe. Koma Saulo anati, Sadzaphedwa lero munthu; pakuti lero Yehova anachita chipulumutso m'Israele. Ndipo Samuele ananena kwa anthuwo, Tiyeni tipite ku Giligala, kukonzanso ufumu kumeneko. Ndipo anthu onse anapita ku Giligala; ndi kumeneko analonga Saulo mfumu pamaso pa Yehova m'Giligala; ndi pamenepo anaphera nsembe zoyamika pamaso pa Yehova; ndi pomwepo Saulo ndi anthu onse a Israele anakondwera kwakukulu. Ndipo Samuele anauza Aisraele onse, kuti, Onani ndinamvera mau anu mwa zonse munalankhula ndi ine, ndipo ndinakulongerani mfumu. Ndipo tsopano, siyi mfumu idzayendabe pamaso panu; ndipo ine ndine wokalamba waimvi; ndipo, onani, ana anga amuna ali nanu, ndipo ine ndinayendabe pamaso panu kuyambira ubwana wanga kufikira lero. Ndikalipo ine; chitani umboni wonditsutsa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa wodzozedwa wake; ndinalanda ng'ombe ya yani? Kapena ndinalanda bulu wa yani? Ndinanyenga yani? Ndinasutsa yani? Ndinalandira m'manja mwa yani chokometsera mlandu kutseka nacho maso anga? Ngati ndinatero ndidzachibwezera kwa inu. Ndipo iwo anati, Simunatinyenga, kapena kutisautsa, kapena kulandira kanthu m'manja mwa wina aliyense. Ndipo iye ananena nao, Yehova ali mboni yanu, ndi wodzozedwa wake ali mboni lero kuti simunapeza kanthu m'dzanja langa. Nati iwo, Iye ali mboni. Ndipo Samuele ananena ndi anthuwo, Yehova ndiye amene anaika Mose ndi Aroni, natulutsanso makolo anu m'dziko la Ejipito. Chifukwa chake tsono, imani pano, kuti ndiweruzane nanu pamaso pa Yehova, anakuchitirani inu ndi makolo anu. Pamene Yakobo anafika ku Ejipito, ndi makolo anu anapemphera kwa Yehova, Yehova anatumiza Mose ndi Aroni, amene anatulutsa makolo anu m'Ejipito, nawakhalitsa pamalo pano. Koma iwowa anaiwala Yehova Mulungu wao, Iye nawapereka m'dzanja la Sisera kazembe wa gulu la Hazori, ndi m'dzanja la Afilisti, ndi m'dzanja la mfumu ya Mowabu, iwo naponyana nao. Ndipo anapemphera kwa Yehova, kuti, Tinachimwa, popeza tinasiya Yehova, ndi kutumikira Abaala ndi Asitaroti, koma mutipulumutse tsopano m'manja a adani anthu, ndipo tidzakutumikirani Inu. Ndipo Yehova anatumiza Yerubaala, ndi Baraki, ndi Yefita, ndi Samuele, napulumutsa inu m'manja mwa adani anu pozungulira ponse, ndipo munakhala mosatekeseka. Ndipo pamene munaona kuti Nahasi mfumu ya ana a Amoni inadza kuponyana nanu, munanena ndi ine, Koma mfumu itiweruze; ngakhale mfumu yanu ndiye Yehova Mulungu wanu. Chifukwa chake siyi mfumu imene munaisankha, imene munandipempha; ndipo taonani, Yehova anakuikirani mfumu. Mukaopa Yehova ndi kumtumikira ndi kumvera mau ake, ndi kusakana lamulo lake la Yehova, ndipo inu ndi mfumu imene iweruza inu mukadzatsata Yehova Mulungu wanu, chabwino. Koma mukapanda kumvera mau a Yehova, ndi kupikisana ndi lamulo la Yehova, dzanja la Yehova lidzatsutsana nanu, monga linatsutsana ndi makolo anu. Chifukwa chake tsono, imani pano, muone chinthu ichi chachikulu Yehova adzachichita pamaso panu. Si nyengo yakumweta tirigu lero kodi? Ndidzaitana kwa Yehova, kuti atumize bingu ndi mvula; ndipo mudzazindikira ndi kuona kuti choipa chanu munachichita pamaso pa Yehova ndi kudzipemphera mfumu, nchachikulu. Momwemo Samuele anaitana kwa Yehova; ndipo Yehova anatumiza bingu ndi mvula tsiku lomwelo; ndipo anthu onse anaopa kwambiri Yehova ndi Samuele. Ndipo anthu onse ananena ndi Samuele, Mupempherere akapolo anu kwa Yehova Mulungu wanu, kuti tingafe; popeza pamwamba pa zoipa zathu zonse tinaonjeza choipa ichi, chakuti tinadzipemphera mfumu. Ndipo Samuele ananena kwa anthuwo, Musaope; munachitadi choipa ichi chonse, koma musaleka kutsata Yehova, koma mutumikire Yehova ndi mtima wanu wonse; musapatukire inu kutsata zinthu zachabe, zosapindulitsa, zosapulumutsa, popeza zili zopanda pake. Pakuti Yehova sadzasiya anthu ake chifukwa cha dzina lake lalikulu; pakuti kudamkomera Yehova kukuyesani inu anthu a Iye yekha. Ndipo inenso, kukhale kutali ndi ine, kuchimwira Yehova ndi kuleka kukupemphererani; koma ndidzakulangizani njira yabwino ndi yolungama. Koma mumuope Yehova, ndi kumtumikira koona, ndi mtima wanu wonse; lingalirani zinthu zazikuluzo Iye ana ku chitirani. Koma mukaumirirabe kuchita choipa, mudzaonongeka, inu ndi mfumu yanu yomwe. Saulo anali ndi zaka makumi atatu pamene anayamba ufumu wake; nakhala mfumu ya Israele zaka ziwiri. Pamenepo Saulo anadzisankhira anthu zikwi zitatu a Israele; zikwi za iwowa zinali ndi Saulo ku Mikimasi, ndi kuphiri la ku Betele; ndi chikwi chimodzi anali ndi Yonatani ku Gibea wa ku Benjamini; ndipo anawauza anthu ena onse amuke ku mahema ao. Ndipo Yonatani anathyola kaboma ka Afilisti lokhala ku Geba, ndipo Afilisti anamva za ichi. Ndipo Saulo analiza lipenga m'dziko monse, nati, Amve Ahebri. Ndipo Aisraele onse anamva kunena kuti Saulo anathyola kaboma ka Afilisti, ndi kuti Afilisti anyansidwa ndi Aisraele. Ndipo anthuwo anasonkhana kwa Saulo ku Giligala. Ndipo Afilisti anasonkhana kuti akamenyane ndi Aisraele, anali nao magaleta zikwi makumi atatu, ndi apakavalo zikwi zisanu ndi chimodzi, ndi anthu akuchuluka monga mchenga wa m'mphepete mwa nyanja. Iwowa anakwera namanga zithando ku Mikimasi kum'mawa kwa Betaveni. Pamene anthu a Israele anazindikira kuti ali m'kupsinjika, pakuti anthuwo anasauka mtima, anthuwo anabisala m'mapanga, ndi m'nkhalango, ndi m'matanthwe, ndi m'malinga, ndi m'maenje. Ndipo Ahebri ena anaoloka Yordani nafika ku dziko la Gadi ndi Giliyadi; koma Saulo akali ku Giligala, ndipo anthu onse anamtsata ndi kunthunthumira. Ndipo iye anatsotsa masiku asanu ndi awiri, monga nthawi anampanga Samuele; koma Samuele sanafike ku Giligala, ndipo anthu anabalalika namsiya Saulo. Pamenepo Saulo anati, Andipatsire kuno nsembe yopsereza, ndi nsembe zoyamika. Ndipo iye anapereka nsembe yopserezayo. Ndipo kunali kuti pakutsiriza iye kupereka nsembe yopserezayo, pomwepo, onani, Samuele anafika. Ndipo Saulo anamchingamira kukamlonjera iye. Ndipo Samuele anati, Mwachitanji? Nati Saulo, Chifukwa ndinaona kuti anthuwo alinkubalalika kundisiya ine, ndi kuti inu simunafika masiku aja tinapangana, ndi kuti Afilisti anasonkhana ku Mikimasi; chifukwa chake ndinati, Afilisti adzatitsikira pano pa Giligala, ndisanapembedze Yehova; potero ndinadzifulumira, ndi kupereka nsembe yopsereza. Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Munachita kopusa; simunasunga lamulo la Yehova Mulungu wanu, limene Iye anakulamulirani; mwenzi Yehova atakhazikitsa nthawi yino ufumu wanu, ukhale pa Israele nthawi yosatha. Koma tsopano ufumu wanu sudzakhala chikhalire; Yehova wadzifunira munthu wa pamtima pake; ndipo Yehova wamuika iye akhale mtsogoleri wa anthu ake, chifukwa inu simunasunga chimene Yehova anakulamulirani. Ndipo Samuele anauka nachoka ku Giligala kunka ku Gibea wa ku Benjamini. Ndipo Saulo anawerenga anthu amene anali naye, monga mazana asanu ndi limodzi. Ndipo Saulo, ndi Yonatani mwana wake, ndi anthu akukhala nao anakhala ku Geba wa ku Benjamini; koma Afilistiwo anali nazo zithando zao ku Mikimasi. Ndipo owawanya anatuluka ku zithando za Afilisti magulu atatu; gulu limodzi linalowa njira yonka ku Ofura, ku dera la Suwala; gulu lina linalowa njira yonka ku Betehoroni; ndi gulu linanso linalowa ku njira ya kumalire, akuyang'ana ku chigwa cha Zeboimu kuchipululuko. Ndipo m'dziko lonse la Israele simunapezeka wosula; popeza Afilisti adati, Kuti Aisraele angadzisulire malupanga kapena mikondo; koma Aisraele onse ankatsikira kwa Afilisti, kuti awasanjire munthu yense chikhasu chake, cholimira chake, nkhwangwa yake, ndi chisenga chake; ndipo mtengo wakukonza makasu, ndi zikhasu ndi makasu a mano unali masekeli awiri mwa atatu ndi mtengo wa nkhwangwazo; ndi kusongola zotwikira unali sekeli imodzi mwa atatu. Chomwecho kunali kuti tsiku lankhondolo sunapezeka mkondo kapena lupanga m'manja a anthu onse anali ndi Saulo ndi Yonatani; koma Saulo yekha ndi Yonatani mwana wake anali nazo. Ndipo a ku kaboma ka Afilisti anatuluka kunja ku mpata wa ku Mikimasi. Ndipo kunali tsiku lina kuti Yonatani mwana wa Saulo ananena ndi mnyamata wonyamula zida zake, Tiye tipite kunka ku kaboma ka Afilisti, tsidya lija. Koma sanauze atate wake. Ndipo Saulo analikukhala m'matsekerezo a Gibea patsinde pa mtengo wankhangaza uli ku Migironi; ndipo panali naye anthu monga mazana asanu ndi limodzi; ndi Ahiya mwana wa Ahitubi mbale wake wa Ikabodi, mwana wa Finehasi, mwana wa Eli, wansembe wa Yehova wa ku Silo, wovala efodi. Ndipo anthuwo sanadziwe kuti Yonatani wachoka. Ndipo pakati pa mipata imene Yonatani anafuna kupitapo kunka ku kaboma ka Afilisti, panali phiri lathanthwe pa mbali ina, ndi phiri lathanthwe pa mbali inzake; ndipo dzina la linalo ndilo Bozezi, ndi la linzake ndilo Sene. Phiri lija linaimirira kuyang'ana kumpoto pandunji pa Mikimasi, ndi linzake kumwera pandunji pa Geba. Ndipo Yonatani ananena ndi mnyamata wonyamula zida zake, Tiye tipite ku kaboma ka osadulidwa awa; kapena Yehova adzatigwirira ntchito; pakuti palibe chomletsa Yehova kupulumutsa angakhale ndi ambiri kapena ndi owerengeka. Ndipo wonyamula zida zake anena naye, Chitani zonse zili mumtima mwanu; palukani, onani ndili pamodzi ndi inu monga mwa mtima wanu. Ndipo Yonatani anati, Taona, ife tidzapita kunka kwa anthuwo, ndipo tidzadziwulula kwa iwo. Akatero ndi ife kuti, Baimani kufikira titsikira kwa inu; tsono tidzaima m'malo mwathu, osakwera kwa iwo. Koma akatero kuti, Kwerani kuno kwa ife, tsono tidzakwera; pakuti Yehova wawapereka m'manja mwathu; ndipo ichi chidzatikhalira chizindikiro. Ndipo onse awiri anadziwulula kwa a ku kaboma ka Afilistiwo; ndipo Afilistiwo anati, Onani, Ahebri alikutuluka m'mauna m'mene anabisala. Ndipo a ku kabomawo anayankha Yonatani ndi wonyamula zida zake, nati, Kwerani kuno kwa ife, tikuonetseni kanthu. Ndipo Yonatani, anauza wonyamula zida zake, Kwera unditsate m'mbuyo, pakuti Yehova wawapereka m'dzanja la Israele. Ndipo Yonatani anakwera chokwawa, ndi wonyamula zida zake anamtsata; ndi Afilisti anagwa pamaso pa Yonatani, ndi wonyamula zida zake anawapha pambuyo pake. Kuwapha koyambako, Yonatani ndi wonyamula zida zake, anapha monga anthu makumi awiri, monga ndime ya munda yolima ng'ombe ziwiri tsiku limodzi. Ndipo kunali kunthunthumira kuzithando, kuthengoko, ndi pakati pa anthu onse; a ku kaboma ndi owawanya omwe ananthunthumira; ndi dziko linagwedezeka; chomwecho kunali kunthunthumira kwakukulu koposa. Ndipo ozonda a Saulo ku Gibea wa ku Benjamini anayang'ana; ndipo, onani, khamu la anthu linamwazikana, kulowa kwina ndi kwina. Pamenepo Saulo ananena ndi anthu amene anali naye, Awerenge tsopano, kuti tizindikire anatichokera ndani. Ndipo pamene anawerenga, onani Yonatani ndi wonyamula zida zake panalibe. Ndipo Saulo ananena ndi Ahiya, Bwera nalo likasa la Mulungu kuno. Pakuti likasa la Mulungu linali kumeneko masiku aja ndi ana a Israele. Ndipo kunali m'mene Saulo anali chilankhulire ndi wansembeyo, phokoso la m'chigono cha Afilisti linachitikabe, nilikula; ndipo Saulo ananena ndi wansembeyo, Bweza dzanja lako. Ndipo Saulo ndi anthu onse amene anali naye anaunjikana pamodzi, natulukira kunkhondoko; ndipo taonani, munthu yense anakantha mnzake ndi lupanga, ndipo panali kusokonezeka kwakukulu. Ndiponso Ahebri akukhala nao Afilisti kale, amene anatuluka m'dziko lozungulira kukalowa nao kuzithando; iwonso anatembenukira kuti akakhale ndi Aisraele amene anali ndi Saulo ndi Yonatani. Anateronso Aisraele onse akubisala m'phiri la Efuremu, pakumva kuti Afilisti anathawa, iwo anawapirikitsa kolimba kunkhondoko. Chomwecho Yehova anapulumutsa Israele tsiku lija; ndipo nkhondo inapitirira pa Betaveni. Ndipo Aisraele anasauka tsiku lija; pakuti Saulo anawalumbirira, kuti, Atembereredwe iye wakudya kanthu kufikira madzulo, ndikabwezere chilango adani anga. Motero anthu onse anakhala opanda kudya. Ndipo anthu onsewo analowa munkhalango, panali uchi pansi. Ndipo pakufika anthuwo m'nkhalangomo, onani, madzi a uchi anachuluka; koma panalibe munthu mmodzi anaika dzanja lake pakamwa, pakuti anthuwo anaopa tembererolo. Koma Yonatani sanamve m'mene atate wake analumbirira anthu; chifukwa chake iye anatambalitsa ndodo ya m'dzanja lake, naitosa m'chisa cha uchi, naika dzanja lake pakamwa pake; ndipo m'maso mwake munayera. Ndipo wina wa anthuwo anayankha, nati, Atate wanu analangiza anthu kolimba ndi lumbiro, ndi kuti, Wotembereredwa iye wakudya lero chakudya. Ndipo anthuwo analema. Ndipo Yonatani anati, Atate wanga wavuta dziko; onani m'maso mwanga mwayera, chifukwa ndinalawako pang'ono uchiwu. Koposa kotani nanga, ngati anthu akadadya nakhuta zowawanya anazipeza za adani ao? Popeza tsopano palibe kuwapha kwakukulu kwa Afilisti. Ndipo anakantha Afilisti tsiku lija kuyambira ku Mikimasi kufikira ku Ayaloni, ndipo anthu anafooka kwambiri. Ndipo anthuwo anathamangira zowawanyazo, natenga nkhosa, ndi ng'ombe, ndi anaang'ombe, naziphera pansi; anthu nazidya zili ndi mwazi wao. Pamenepo anauza Saulo, kuti, Onani anthu alikuchimwira Yehova, umo akudya zamwazi. Ndipo iye anati, Munachita konyenga; kunkhunizani mwala waukulu kwa ine lero. Ndipo Saulo anati, Balalikani pakati pa anthu, nimuwauze kuti abwere kwa ine kuno munthu yense ndi ng'ombe yake, ndi munthu yense ndi nkhosa yake, aziphe pano, ndi kuzidya, osachimwira Yehova ndi kudya zamwazi. Nabwera anthu onse, yense ndi ng'ombe yake, usiku uja naziphera pomwepo. Ndipo Saulo anamangira Yehova guwa la nsembe; limenelo ndilo guwa loyamba iye anamangira Yehova. Ndipo Saulo anati, Tiyeni titsikire usiku kwa Afilistiwo, ndi kuwawawanya kufikira kutayera, tisasiye munthu mmodzi wa iwowa. Ndipo iwo anati, Chitani chilichonse chikukomerani. Pamenepo wansembeyo anati, Tisendere kwa Yehova kuno. Ndipo Saulo anafunsira uphungu kwa Mulungu, Nditsikire kodi kwa Afilisti? Mudzawapereka m'dzanja la Israele kodi? Koma Iye sanamyankhe tsiku lomweli. Ndipo Saulo anati, Musendere kuno, inu nonse akulu a anthu; kuti muzindikire ndi kuona m'mene muli choipa ichi lero. Pakuti, pali Yehova wakupulumutsa Israele, chingakhale chili m'mwana wanga Yonatani, koma adzafa ndithu. Koma pakati pa anthu onse panalibe mmodzi wakumyankha iye. Ndipo iye ananena ndi Aisraele onse, Inu mukhale mbali ina, ndipo ine ndi Yonatani mwana wanga tidzakhala mbali yinanso. Ndipo anthuwo ananena ndi Saulo, Chitani chimene chikukomerani. Chifukwa chake Saulo ananena ndi Yehova, Mulungu wa Israele, muonetse choonadi. Ndipo maere anagwera Saulo ndi Yonatani; koma anthuwo anapulumuka. Ndipo Saulo anati, Muchite maere pakati pa ine ndi Yonatani mwana wanga. Ndipo anagwera Yonatani. Pamenepo Saulo ananena ndi Yonatani, Undiuze chimene unachita. Ndipo Yonatani anamuuza, nati, Zoonadi ndinangolawako uchi pang'ono ndi nsonga ya ndodo inali m'dzanja langa: ndipo onani ndiyenera kufa. Pamenepo Saulo anati, Mulungu andilange, naonjezereko, pakuti udzafa ndithu, Yonatani. Ndipo anthuwo ananena ndi Saulo, kodi Yonatani adzafa, amene anachititsa chipulumutso chachikulu ichi m'Israele? Musatero. Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la pa mutu wake lidzagwa pansi, pakuti iye anagwirizana ndi Mulungu lero. Chomwecho anthuwo anapulumutsa Yonatani kuti angafe. Ndipo Saulo analeka kuwapirikitsa Afilistiwo; ndi Afilistiwo anamuka ku malo a iwo okha. Ndipo pamene Saulo atakhazikitsa ufumu wa pa Israele, iye anaponyana ndi adani ake onse pozungulira ponse, ndi Mowabu, ndi ana a Amoni, ndi Edomu ndi mafumu a Zoba, ndi Afilisti; ndipo paliponse anapotolokerapo, anawalanga. Ndipo iye anakula mphamvu, nakantha Aamaleke, napulumutsa Aisraele m'manja a akuwawawanya. Ndipo ana a Saulo ndiwo Yonatani, ndi Isivi, ndi Malikisuwa; ndi maina a ana akazi ake awiri ndi awa: dzina la woyamba ndiye Merabi, ndi dzina la mng'ono wake ndiye Mikala; ndi dzina la mkazi wa Saulo ndi Ahinowamu mwana wa Ahimaazi; ndi dzina la kazembe wa khamu lankhondo lake ndiye Abinere mwana wa Nere, mbale wake wa atate wa Saulo. Ndipo atate wa Saulo ndiye Kisi; ndipo Nere atate wa Abinere ndiye mwana wa Abiyele. Ndipo panali nkhondo yowawa ndi Afilisti masiku onse a Saulo; ndipo Saulo pakuona munthu wamphamvu, kapena ngwazi, anamtenga akhale naye. Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Yehova ananditumiza ine kukudzozani mukhale mfumu ya anthu ake Aisraele; chifukwa chake tsono mumvere kunena kwa mau a Yehova. Atero Yehova wa makamu, Ndinaonerera chimene Amaleke anachitira Israele, umo anamlalira panjira, m'mene iye anakwera kutuluka m'Ejipito. Muka tsopano, nukanthe Amaleke, nuononge konsekonse zonse ali nazo, usawalekerere, koma uwaphe mwamuna ndi mkazi, mwana ndi woyamwa, ng'ombe ndi nkhosa, ngamira ndi bulu. Ndipo Saulo anamemeza anthu, nawawerenga ku Telaimu, akuyenda pansi zikwi mazana awiri, ndi a kwa Yuda anthu zikwi khumi. Ndipo Saulo anafika kumudzi wa Amaleke, nalalira kuchigwa. Ndipo Saulo anauza Akeni kuti, Mukani, chokani mutsike kutuluka pakati pa Aamaleke, kuti ndingakuonongeni pamodzi ndi iwo; pakuti inu munachitira ana a Israele onse zabwino, pakufuma iwo ku Ejipito. Chomwecho Akeni anachoka pakati pa Aamaleke. Ndipo Saulo anakantha Aamaleke, kuyambira pa Havila, dera la ku Suri, chili pandunji pa Ejipito. Namtenga wamoyo Agagi, mfumu ya Aamaleke, naononga konsekonse anthu onse ndi lupanga lakuthwa. Koma Saulo ndi anthu anamsunga wamoyo Agagi, ndi nkhosa zokometsetsa, ndi ng'ombe, ndi zonenepa zina, ndi anaankhosa, ndi zabwino zonse sadafuna kuzitha psiti; koma zonse zoipa ndi zonyansa anaziononga konsekonse. Pamenepo mau a Yehova anafika kwa Samuele, nati, Kundichititsa chisoni kuti ndinaika Saulo akhale mfumu; pakuti wabwerera wosanditsata Ine, ndipo sanachite malamulo anga. Ndipo Samuele anakwiya; nalira kwa Yehova usiku wonse. Ndipo Samuele analawirira m'mawa kuti akakomane ndi Saulo; ndipo munthu anamuuza Samuele kuti, Saulo anafika ku Karimele, ndipo taonani, anaimika chikumbutso chake, nazungulira, napitirira, natsikira ku Giligala. Ndipo Samuele anadza kwa Saulo; ndipo Saulo anati kwa iye, Yehova akudalitseni; ine ndinachita lamulo la Yehova. Ndipo Samuele anati, Koma tsono kulirako kwa nkhosa ndilikumva m'makutu anga, ndi kulirako kwa ng'ombe ndilikumva, nchiyani? Ndipo Saulo anati, Anazitenga kwa Aamaleke; pakuti anthu anasunga nkhosa zokometsetsa ndi ng'ombe, kuzipereka nsembe kwa Yehova Mulungu wanu; koma zina tinaziononga konsekonse. Pomwepo Samuele ananena ndi Saulo, Imani, ndidzakudziwitsani chimene Yehova wanena ndi ine usiku walero. Ndipo iyeyo anati kwa iye, Nenani. Nati Samuele, M'mene munali wamng'ono m'maso a inu nokha, kodi simunaikidwa mutu wa mafuko a Israele? Ndipo Yehova anakudzozani mfumu ya Israele. Ndipo Yehova anakutumani ulendo, kuti, Muka, nuononge konsekonse Aamaleke akuchita zoipawo, nuponyane nao kufikira utawatha. Chifukwa ninji tsono simunamvera mau a Yehova, koma munathamangira zowawanya, ndi kuchita choipa pamaso pa Yehova? Ndipo Saulo ananena ndi Samuele, Koma ndinamvera mau a Yehova, ndipo ndinayenda njira Yehova anandituma ine, ndipo ndinabwera naye Agagi mfumu ya Amaleke, ndi Aamaleke ndinawaononga konsekonse. Koma anthuwo anatengako zowawanya, nkhosa ndi ng'ombe, zoposa za zija tidayenera kuziononga, kuziphera nsembe kwa Yehova Mulungu wanu ku Giligala. Ndipo Samuele anati, Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mau a Yehova? Taonani, kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kutchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo. Pakuti kupanduka kuli ngati choipa cha kuchita nyanga, ndi mtima waliuma uli ngati kupembedza milungu yachabe ndi maula. Popeza inu munakaniza mau a Yehova, Iyenso anakaniza inu, kuti simudzakhalanso mfumu. Ndipo Saulo anati kwa Samuele, Ndinachimwa; pakuti ndinalumpha lamulo la Yehova, ndi mau anu omwe; chifukwa ndinaopa anthuwo, ndi kumvera mau ao. Chifukwa chake tsono, mukhululukire tchimo langa, nimubwerere pamodzi ndi ine, kuti ndikalambire Yehova. Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Ine sindibwerera nanu; pakuti munakaniza mau a Yehova, ndipo Yehova anakaniza inu, kuti simudzakhalanso mfumu ya Israele. Ndipo pakupotoloka Samuele kuti achoke, iye anagwira chilezi cha mwinjiro wake, ndipo chinang'ambika. Ndipo Samuele ananena naye, Yehova anang'amba ufumu wa Israele lero kuuchotsa kwa inu, naupatsa kwa mnansi wanu wina wabwino woposa inu. Ndiponso Wamphamvu wa Israele sanama kapena kulapa; popeza Iye sali munthu kuti akalapa. Pomwepo iye anati, Ndinachimwa, koma mundichitire ulemu tsopano pamaso pa akulu a anthu anga, ndi pamaso pa Israele, nimubwerere pamodzi ndi ine, kuti ndikalambire Yehova Mulungu wanu. Chomwecho Samuele anabwerera natsata Saulo; ndi Saulo analambira Yehova. Ndipo Samuele anati, Bwerani naye kwa ine kuno Agagi mfumu ya Aamaleke. Ndipo Agagi anabwera kwa iye mokondwera. Nati Agagi, Zoonadi kuwawa kwa imfa kunapitirira. Ndipo Samuele anati, Monga lupanga lako linachititsa akazi ufedwa, momwemo mai wako adzakhala mfedwa mwa akazi. Ndipo Samuele anamdula Agagi nthulinthuli pamaso pa Yehova ku Giligala. Pamenepo Samuele ananka ku Rama; ndi Saulo anakwera kunka kunyumba yake ku Gibea wa Saulo. Ndipo Samuele sanadzenso kudzaona Saulo kufikira tsiku la imfa yake; koma Samuele analira chifukwa cha Saulo; ndipo Yehova anali ndi chisoni kuti anamlonga Saulo mfumu ya Israele. Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Iwe ukuti ulire chifukwa cha Saulo nthawi yotani, popeza Ine ndinamkana kuti asakhale mfumu ya Israele? Dzaza nyanga yako ndi mafuta, numuke, ndidzakutumiza kwa Yese wa ku Betelehemu; pakuti ndinadzionera mfumu pakati pa ana ake. Ndipo Samuele anati, Ndikamuka bwanji? Saulo akachimva, adzandipha. Ndipo Yehova anati, Umuke nayo ng'ombe yaikazi, nunene kuti, Ndadza kudzaphera nsembe kwa Yehova. Ndipo uitane Yese abwere kunsembeko, ndipo Ine ndidzakusonyeza chimene uyenera kuchita; ndipo udzandidzozera iye amene ndidzakutchulira dzina lake. Ndipo Samuele anachita chimene Yehova ananena, nadza ku Betelehemu. Ndipo akulu a mudziwo anadza kukomana naye monthunthumira, nati, Mubwera ndi mtendere kodi? Nati iye, Ndi mtendere umene; ndadza kudzaphera nsembe kwa Yehova; mudzipatule ndi kufika ndi ine kunsembeko. Ndipo iye anapatula Yese ndi ana ake, nawaitanira kunsembeko. Ndipo kunali, pakufika iwo, iye anayang'ana pa Eliyabu, nati, Zoonadi, wodzozedwa wa Yehova ali pamaso pake. Koma Yehova ananena ndi Samuele, Usayang'ane nkhope yake, kapena kutalika kwa msinkhu wake, popeza Ine ndinamkana iye; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang'ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang'ana mumtima. Pamenepo Yese anaitana Abinadabu nampititsa pa Samuele. Ndipo iye adati, Koma uyunso Yehova sadamsankhe. Pamenepo Yese anapititsapo Sama. Ndipo anati, Koma uyunso Yehova sanamsankhe. Ndipo Yese anapititsapo ana ake amuna asanu ndi awiri. Koma Samuele anati kwa Yese, Yehova sanawasankhe awa. Ndipo Samuele anati kwa Yese, Ana anu ndi omwewa kodi? Nati iye, Watsala wina, mng'ono wa onse, ndipo taonani, iye alikuweta nkhosa. Ndipo Samuele anati kwa Yese, Tumiza munthu akamtenge; pakuti ife sitidzakhala pansi kufikira iye atadza kuno. Ndipo anatumiza munthu, nabwera naye. Tsono iye anali wofiirira, ndi wa nkhope yokongola, ndi maonekedwe okoma. Ndipo Yehova anati, Nyamuka umdzoze, pakuti ndi ameneyu. Pamenepo Samuele anatenga nyanga ya mafuta, namdzoza pakati pa abale ake; ndipo mzimu wa Yehova unalimbika pa Davide kuyambira tsiku lomweli. Ndipo Samuele ananyamuka, nanka ku Rama. Koma mzimu wa Yehova unamchokera Saulo, ndi mzimu woipa wochokera kwa Yehova unamvuta iye. Ndipo anyamata a Saulo ananena naye, Onani tsopano, mzimu woipa wochokera kwa Mulungu ulikuvuta inu. Tsono inu mbuye wathu muuze anyamata anu, amene ali pamaso panu, kuti afune munthu wanthetemya wodziwa kuimba zeze; ndipo kudzakhala, pamene mzimu woipa wochokera kwa Mulungu uli pa inu, iyeyo adzaimba ndi dzanja lake, ndipo mudzakhala wolama. Ndipo Saulo anati kwa anyamata ake, Mundifunire tsono munthu wakudziwa kuimba bwino, nimubwere naye kwa ine. Ndipo mnyamata wake wina anayankha, nati, Taonani, ine ndaona mwana wa Yese wa ku Betelehemu, ndiye wanthetemya wodziwa kuimbira, ndipo ali wa mtima wolimba ndi woyenera nkhondo, ndiponso ali wochenjera manenedwe ake; ndiye munthu wokongola, ndipo Yehova ali naye. Chifukwa chake Saulo anatumiza mithenga kwa Yese, nati, Unditumizire Davide, mwana wako, amene ali kunkhosa. Ndipo Yese anatenga bulu namsenza mkate, ndi thumba la vinyo, ndi mwanawambuzi, nazitumiza kwa Saulo ndi Davide mwana wake. Ndipo Davide anafika kwa Saulo, naima pamaso pake; ndipo iye anamkonda kwambiri, namsandutsa wonyamula zida zake. Ndipo Saulo anatumiza kwa Yese, nati, Ulole kuti Davide aime pamaso panga; pakuti ndamkomera mtima. Ndipo kunali kuti pamene mzimu woipawo wochokera kwa Mulungu unali pa Saulo, Davide anatenga zeze, naliza ndi dzanja lake; chomwecho Saulo anatsitsimuka, nakhala bwino, ndi mzimu woipa unamchokera iye. Pamenepo Afilisti anasonkhanitsa makamu ao a nkhondo, naunjikana ku Soko wa ku Yuda, namanga zithando pakati pa Soko ndi Azeka ku Efesi-Damimu. Ndipo Saulo ndi anthu a Israele anasonkhana, namanga zithando pa chigwa cha Ela, nandandalitsa nkhondo yao kuti akaponyane ndi Afilisti. Ndipo Afilisti anaima paphiri tsidya lija, ndi Aisraele anaima paphiri tsidya lina; ndi pakati pao panali chigwa. Ndipo ku zithando za Afilisti kunatuluka chiwinda, dzina lake Goliyati wa ku Gati, kutalika kwake ndiko mikono isanu ndi umodzi ndi dzanja limodzi. Ndipo anali ndi chisoti chamkuwa pamutu pake, navala malaya aunyolo, olemera ngati masekeli zikwi zisanu za mkuwa, nakuta msongolo wake ndi chovala chamkuwa, ndiponso pachikota pake panali nthungo yamkuwa. Ndipo mtengo wa mkondo wake unali ngati mtanda woombera nsalu; ndi khali la mkondowo linalemera ngati masekeli mazana asanu ndi limodzi a chitsulo; ndipo womnyamulira chikopa anamtsogolera. Naima iye naitana makamu a nkhondo a Israele, nanena nao, Munatulukiranji kundandalitsa nkhondo yanu? Sindine Mfilisti kodi, ndi inu anyamata a Saulo? Mudzisankhire munthu, atsikire kwa ine. Akakhoza iyeyo kuponyana ndi ine ndi kundipha, tidzakhala ife akapolo anu; koma ine ndikamlaka, ndi kumupha, tsono mudzakhala inu akapolo athu, ndi kutitumikira ife. Nati Mfilistiyo, Ine ndinyoza makamu a nkhondo a Israele lero; mundipatse munthu, kuti tilimbane ife awiri. Ndipo pamene Saulo ndi Aisraele onse anamva mau ao a Mfilistiyo, anadodoma, naopa kwambiri. Tsono Davide anali mwana wa Mwefurati uja wa ku Betelehemu-Yuda, dzina lake ndiye Yese; ameneyu anali nao ana amuna asanu ndi atatu; ndipo m'masiku a Saulo munthuyo anali nkhalamba, mwa anthu. Ndipo ana atatu akulu a Yese anatsata Saulo kunkhondoko; ndi maina ao a ana ake atatuwo adapita ku nkhondowo ndiwo Eliyabu woyambayo, ndi mnzake womponda pamutu pake Abinadabu, ndi wachitatu Sama. Ndipo Davide anali wotsiriza; ndi akulu atatuwo anamtsata Saulo. Koma Davide akamuka kwa Saulo, nabwerera kudzadyetsa nkhosa za atate wake ku Betelehemu. Ndipo Mfilistiyo anayandikira m'mawa ndi madzulo, nadzionetsera masiku makumi anai. Ndipo Yese anati kwa Davide mwana wake, Uwatengere abale ako efa wa tirigu uyu wokazinga, ndi mikate iyi khumi, nuthamangire nazo kuzithando kwa abale ako; nunyamule nchinchi izi khumi zamase ukapatse mtsogoleri wa chikwi chao, nukaone m'mene akhalira abale ako, nulandire chikole chao. Tsono Saulo, ndi iwowa, ndi anthu onse a Israele, anali m'chigwa cha Ela, ku nkhondo ya Afilisti. Ndipo Davide anauka m'mamawa, nasiyira nkhosa wozisungira, nasenza zija, namuka, monga anamuuza Yese; ndipo iye anafika ku linga la magaleta, napeza khamu lilikutuluka kunka poponyanira nkhondo lilikufuula. Ndipo Israele ndi Afilisti anandandalitsa nkhondo zao, khamu lina kuyang'anana ndi khamu lina. Ndipo Davide anasiya akatundu ake m'dzanja la wosungira akatundu, nathamangira ku khamulo, nadza nawalonjera abale ake. Ndipo m'mene iye anali chilankhulire nao, onani chinakwerako chiwindacho, Mfilisti wa ku Gati, dzina lake Goliyati, wotuluka pakati pa mipambo ya Afilisti, nalankhula monga mau omwe aja; ndipo Davide anawamva. Ndipo Aisraele onse, pakumuona munthuyo, anamthawa, naopa kwambiri. Nati Aisraele, Kodi mwaona munthu uyu amene anakwera kuno? Zoonadi iye anakwera kuti adzanyoze Israele, ndipo munthu wakumupha iye, mfumu idzamlemeza ndi chuma chambiri, nidzampatsa mwana wake wamkazi, nidzayesa nyumba ya atate wake yaufulu m'Israele. Ndipo Davide analankhula ndi anthu akuima pafupi ndi iye, nati, Adzamchitira chiyani munthu wakupha Mfilisti uyu, ndi kuchotsa tonzo lake pakati pa Israele? Pakuti Mfilisti uyu wosadulidwa ndiye yani, kuti azinyoza makamu a Mulungu wamoyo? Ndipo anthuwo anamyankha motero, nati, Adzamchitira munthu wakumupha iye mwakutimwakuti. Ndipo Eliabu mkulu wake anamumva iye alikulankhula ndi anthu; ndipo Eliyabu anapsa mtima ndi Davide, nati, Unatsikiranji kuno? Ndi nkhosa zija zowerengeka unazisiya ndi yani, m'chipululu muja? Ine ndidziwa kudzikuza kwako ndi kuipa kwa mtima wako; pakuti watsika kuti udzaone nkhondoyi. Ndipo Davide anati, Ndachitanji tsopano? Palibe chifukwa kodi? Napotolokera iye kwa munthu wina, nalankhula mau omwewo; ndipo anthu anamyankhanso monga momwemo. Ndipo pamene mau adanena Davide anamveka, anawapitiriza kwa Saulo; ndipo iye anamuitana. Ndipo Davide anati kwa Saulo, Asade nkhawa munthu aliyense chifukwa cha iyeyo; ine kapolo wanu ndidzapita kuponyana ndi Mfilisti uyu. Ndipo Saulo anati kwa Davide, Sukhoza iwe kukomana ndi Mfilisti uyu kukaponyana naye; pakuti iwe ndiwe mnyamata, koma iye anazolowera nkhondo kuyambira ubwana wake. Ndipo Davide anati kwa Saulo, Ine kapolo wanu ndinalikusunga nkhosa za atate wanga; ndipo pakubwera mkango, mwina chimbalangondo ndi kutenga nkhosa ya gululo, ndinachithamangira, ndi kuchikantha, ndi kuitulutsa m'kamwa mwake; ndipo pamene chinandiukira, ndinagwira tchowa lake ndi kuchikantha ndi kuchipha. Ine kapolo wanu ndinapha mkango ndi chimbalangondo zonse ziwiri; ndipo Mfilisti uyu wosadulidwa adzakhala ngati mmodzi wa izo, popeza wanyoza makamu a Mulungu wamoyo. Nati Davide, Yehova wakundipulumutsa pa mphamvu ya mkango, ndi mphamvu ya chimbalangondo, Iyeyu adzandipulumutsa m'dzanja la Mfilisti uyu. Ndipo Saulo anati kwa Davide, Muka, Yehova akhale nawe. Ndipo Saulo anaveka Davide zovala zake za iye yekha, namveka chisoti chamkuwa pamutu pake, namvekanso malaya aunyolo. Ndipo Davide anamanga lupanga lake pamwamba pa zovala zake, nayesa kuyenda nazo; popeza sanaziyesera kale. Ndipo Davide anati kwa Saulo, Sindikhoza kuyenda ndi izi; pakuti sindinazizolowera. Nazivula Davide. Natenga ndodo yake m'dzanja lake nadzisankhira miyala isanu yosalala ya mumtsinje, naiika m'thumba la kubusa, limene anali nalo ndilo chibete; ndi choponyera miyala chinali m'dzanja lake, momwemo anayandikira kwa Mfilistiyo. Ndipo Mfilistiyo anadza, nayandikira kwa Davide; ndi wonyamula chikopa chake anamtsogolera. Ndipo Mfilisti pakumwazamwaza maso, ndi kuona Davide, anampeputsa; popeza anali mnyamata chabe, wofiirira, ndi wa nkhope yokongola. Ndipo Mfilisti anati kwa Davide, Ine ndine galu kodi, kuti iwe ukudza kwa ine ndi ndodo? Ndi Mfilistiyo anatukwana Davide natchula milungu yake. Ndipo Mfilistiyo anati kwa Davide, Idza kuno kwa ine, ndidzapatsa mnofu wako kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zilombo za kuthengo. Ndipo Davide anati kwa Mfilistiyo, Iwe ukudza kwa ine ndi lupanga, ndi mkondo, ndi nthungo; koma ine ndafika kwa iwe m'dzina la Yehova wa makamu, Mulungu wa ankhondo a Israele amene iwe unawanyoza. Lero lino Yehova adzakupereka iwe m'dzanja langa, ndipo ndidzakukantha, ndi kukuchotsera mutu wako. Ndipo lero ndidzapatsa mitembo ya makamu a Afilisti kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zilombo za dziko lapansi; kuti dziko lonse likazindikire kuti kwa Israele kuli Mulungu. Ndi msonkhano wonse uno udzazindikira kuti Yehova sapulumutsa ndi lupanga, kapena ndi mkondo; pakuti Yehova ndiye mwini nkhondo, ndipo Iye adzakuperekani inu m'manja athu. Ndipo kunali, pamene Mfilistiyo anadzikonza, nadza, nasendera pafupi kuti akomane ndi Davide, Davide anafulumira, nathamangira ku khamulo, kuti akomane ndi Mfilistiyo. Ndipo Davide anapisa dzanja lake m'thumba mwake, natulutsamo mwala, nauponya, nalasa Mfilistiyo pamphumi; ndi mwalawo unalowa m'mphumi, ndipo iye anagwa pansi chafufumimba. Chomwecho Davide anapambana Mfilistiyo ndi mwala wa choponyera chake, nakantha Mfilistiyo, namupha. Koma m'dzanja la Davide munalibe lupanga. Potero Davide anathamanga naima pa Mfilistiyo, nagwira lupanga lake, nalisolola m'chimake, namtsiriza nadula nalo mutu wake. Ndipo pakuona Afilisti kuti chiwinda chao chidafa, anathawa. Ndipo anthu a Israele ndi Ayuda ananyamuka, nafuula, nathamangira Afilistiwo, mpaka ufika kuchigwako, ndi ku zipata za Ekeroni. Ndipo Afilistiwo olasidwa anagwa pa njira ya ku Saaraimu, kufikira ku Gati ndi ku Ekeroni. Ndipo ana a Israele atathamangira Afilisti, anabwerera nafunkha za m'zithando zao. Ndipo Davide anatenga mutu wa Mfilistiyo, napita nao ku Yerusalemu; koma zida zake anazisunga m'hema wake. Ndipo pamene Saulo anaona Davide alikutulukira kwa Mfilistiyo, iye anati kwa Abinere, kazembe wa khamu la nkhondo, Abinere, mnyamata uyu ndi mwana wa yani? Nati Abinere, Pali moyo wanu, mfumu, ngati ndidziwa. Ndipo mfumu inati, Ufunsire kuti mnyamatayo ndi mwana wa yani. Ndipo pamene Davide anabwera, atapha Mfilistiyo, Abinere anamtenga, nafika naye pamaso pa Saulo, mutu wa Mfilistiyo uli m'dzanja lake. Ndipo Saulo anati kwa iye, Mnyamata iwe, ndiwe mwana wa yani? Davide nayankha, Ndili mwana wa kapolo wanu Yese wa ku Betelehemu. Ndipo kunali, pakutsiriza iye kulankhula ndi Saulo, mtima wa Yonatani unalumikizika ndi mtima wa Davide, ndipo Yonatani anamkonda iye monga moyo wa iye yekha. Ndipo Saulo anamtenga tsiku lomwelo, osamlolanso apite kwao kwa atate wake. Pamenepo Yonatani ndi Davide anapangana pangano, pakuti adamkonda iye ngati moyo wa iye yekha. Ndipo Yonatani anavula malaya ake anali nao, napatsa Davide, ndi zovala zake, ngakhale lupanga lake, ndi uta wake, ndi lamba lake. Ndipo Davide anatuluka kunka kulikonse Saulo anamtumako, nakhala wochenjera; ndipo Saulo anamuika akhale woyang'anira anthu a nkhondo; ndipo ichi chinakomera anthu onse, ndi anyamata a Saulo omwe. Ndipo kunali pakudza iwo, pamene Davide anabwera atapha Afilistiwo, anthu akazi anatuluka m'midzi yonse ya Israele, ndi kuimba ndi kuvina, kuti akakomane ndi mfumu Saulo, ndi malingaka, ndi chimwemwe, ndi zoimbira. Ndipo akazi anathirirana mang'ombe m'kuimba kwao, nati, Saulo anapha zikwi zake, koma Davide zikwi zake zankhani. Koma Saulo anakwiya ndithu, ndi kunenaku kunamuipira; nati, Kwa Davide anawerengera zikwi zankhani, koma kwa ine zikwi zokha; chimperewera nchiyaninso, koma ufumu wokha? Ndipo kuyambira tsiku lomwelo ndi m'tsogolo mwake, Saulo anakhala maso pa Davide. Ndipo kunali m'mawa mwake, mzimu woipa wochokera kwa Mulungu unamgwira Saulo mwamphamvu, iye nalankhula moyaluka m'nyumba yake; koma Davide anaimba ndi dzanja lake, monga amachita tsiku ndi tsiku; koma m'dzanja la Saulo munali mkondo. Ndipo Saulo anaponya mkondowo; pakuti anati, Ndidzapyoza Davide ndi kumphatikiza ndi khoma. Ndipo Davide analewa kawiri kuchoka pamaso pake. Ndipo Saulo anaopa Davide chifukwa Yehova anali naye, koma adamchokera Saulo. Chifukwa chake Saulo anamchotsa kuti asakhale naye, namuika akhale mtsogoleri wake wa anthu chikwi chimodzi; ndipo iye anatsogolera anthu kutuluka ndi kubwera nao. Ndipo Davide anakhala wochenjera m'mayendedwe ake onse; ndipo Yehova anali naye. Ndipo pamene Saulo anaona kuti analikukhala wochenjera ndithu anamuopa. Koma Aisraele onse ndi Ayuda onse anamkonda Davide pakuti anawatsogolera kutuluka ndi kulowa nao. Ndipo Saulo anati kwa Davide, Ona, mwana wanga wamkazi wamkulu, dzina lake Merabi, iyeyo ndidzakupatsa akhale mkazi wako; koma undikhalire ngwazi, nuponye nkhondo za Yehova. Pakuti Saulo anati, Dzanja langa lisamkhudze, koma dzanja la Afilisti ndilo. Ndipo Davide anati kwa Saulo, Ine ndiye yani, ndi moyo wanga uli wotani, kapena banja la atate wanga lili lotani m'Israele, kuti ine ndidzakhala mkamwini wa mfumu? Koma kunali nthawi imene akadapatsa Merabi mwana wamkazi wa Saulo kwa Davide, iye anapatsidwa kwa Adriyele Mmehola kukhala mkazi wake. Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Saulo anakonda Davide; ndipo pakumva Saulo, anakondwera nako. Nati Saulo, Ndidzampatsa iye, kuti amkhalire msampha, ndi kuti dzanja la Afilisti limgwere. Chifukwa chake Saulo ananena ndi Davide, Lero udzakhala mkamwini wanga kachiwiri. Ndipo Saulo analamulira anyamata ake, nati, Mulankhule naye Davide m'tseri, ndi kuti, Taonani mfumu akondwera nanu, ndi anyamata ake onse akukondani; chifukwa chake tsono, khalani mkamwini wa mfumu. Ndipo anyamata a Saulo analankhula mau awa m'makutu a Davide. Nati Davide, Kodi muchiyesera chinthu chopepuka kukhala mkamwini wa mfumu, popeza ndili munthu wosauka, ndi wopeputsidwa. Ndipo anyamata a Saulo anamuuza, kuti, Anatero Davide. Nati Saulo, Mudzatero kwa Davide, kuti mfumu safuna cholowolera china, koma nsonga za makungu zana limodzi za Afilisti, kuti abwezere chilango adani a mfumu. Koma Saulo anaganizira kupha Davide ndi dzanja la Afilisti. Ndipo pamene anyamata ake anauza Davide mau awa, kudamkomera Davide kukhala mkamwini wa mfumu. Ndipo asanathe masikuwo, ananyamuka Davide, ndi anthu ake, nakaphako Afilisti mazana awiri, ndipo Davide anatenga nsonga za makungu ao nazipatsa mofikira kwa mfumu, kuti akhale mkamwini wa mfumu. Ndipo Saulo anampatsa Mikala mwana wake wamkazi akhale mkazi wake. Ndipo Saulo anaona, nadziwa kuti Yehova ali ndi Davide; ndi kuti Mikala mwana wa Saulo anamkonda Davide. Saulo nayamba kumuopa Davide kopambana; ndi Saulo anali mdani wa Davide masiku onse. Pomwepo mafumu a Afilisti anatuluka; ndipo nthawi zonse anatuluka iwo, Davide anali wochenjera koposa anyamata onse a Saulo, chomwecho dzina lake linatamidwa kwambiri. Ndipo Saulo analankhula kwa Yonatani mwana wake, ndi anyamata ake onse kuti amuphe Davide. Koma Yonatani mwana wa Saulo anakondwera kwambiri ndi Davide. Ndipo Yonatani anauza Davide, nati, Saulo atate wanga alikufuna kukupha; chifukwa chake tsono uchenjere m'mawa, mukhale m'malo mosadziwika, nubisale; ndipo ine ndidzakutuluka ndi kuima pa mbali ya atate wanga kumunda kumene kuli iwe, ndipo ndidzalankhula ndi atate wanga za iwe; ndipo ndikaona kanthu ndidzakudziwitsa. Ndipo Yonatani analankhula ndi Saulo atate wake movomereza Davide, nanena naye, Mfumu asachimwire mnyamata wake Davide; chifukwa iyeyo sanachimwire inu, ndipo ntchito zake anakuchitirani zinali zabwino ndithu; popeza iye anataya moyo wake nakantha Mfilistiyo, ndipo Yehova anachitira Aisraele onse chipulumutso chachikulu, inu munachiona, nimunakondwera; tsono mudzachimwiranji mwazi wosalakwa, ndi kumupha Davide popanda chifukwa? Ndipo Saulo anamvera mau a Yonatani; nalumbira, Pali Yehova, sadzaphedwa iye. Pamenepo Yonatani anaitana Davide, namuuza zonsezi. Ndipo Yonatani anafika naye Davide kwa Saulo, iye nakhalanso pamaso pake monga kale. Ndipo kunalinso nkhondo; ndipo Davide anatuluka, nakamenyana ndi Afilisti, nawapha ndi maphedwe akulu, ndipo iwo anamthawa iye. Ndipo mzimu woipa wochokera kwa Yehova unali pa Saulo, pakukhala iye m'nyumba mwake, ndi mkondo wake m'dzanja lake; ndipo Davide anaimba ndi dzanja lake. Ndipo Saulo anayesa kupyoza Davide kumphatikiza kukhoma ndi mkondowo; koma iye anadzilanditsa kuchoka pamaso pa Saulo; ndipo analasa khoma; ndipo Davide anathawa napulumuka usiku uja. Ndipo Saulo anatumiza mithenga kunyumba ya Davide imdikire, ndi kumupha m'mawa; koma Mikala mkazi wa Davide anamuuza, nati, Ukapanda kupulumutsa moyo wako usiku uno, udzaphedwa ndithu m'mawa. Chomwecho Mikala anamtsitsira Davide pazenera, namuka iye, nathawa, napulumuka. Ndipo Mikala anatenga chifanizo nachiika pakama, naika mtsamiro wa ubweya wa mbuzi kumutu kwake, nachifunda zofunda. Ndipo pamene Saulo anatumiza mithenga kuti ikamgwire Davide, anati, Iye alikudwala. Ndipo Saulo anatumiza mithengayo kuti ikaone Davide, nati, Mumtengere iye pa kama wake, kuti ndidzamuphe. Ndipo pakulowa mithengayo, onani, pakama pali chifanizo ndi mtsamiro wa ubweya wa mbuzi kumutu kwake. Nati Saulo kwa Mikala, Wandinyengeranji chomwechi, ndi kulola mdani wanga apulumuke? Ndipo Mikala anayankha Saulo, Iye anati kwa ine, Undilole ndipite, ndingakuphe. Chomwecho anathawa Davide, napulumuka, nafika kwa Samuele ku Rama, namuuza zonse Saulo anamchitira. Ndipo iye ndi Samuele anakhala ku Nayoti. Ndipo wina anauza Saulo, kuti, Onani Davide ali ku Nayoti m'Rama. Ndipo Saulo anatumiza mithenga kuti igwire Davide, ndipo pamene inaona gulu la aneneri alikunenera, ndi Samuele mkulu wao alikuimapo, mzimu wa Mulungu unagwera mithenga ya Saulo, ninenera iyonso. Ndipo pamene anauza Saulo, iye anatumiza mithenga ina; koma iyonso inanenera. Ndipo Saulo anatumiza mithenga kachitatu, nayonso inanenera. Pamenepo iyenso anamuka ku Rama, nafika ku chitsime chachikulu chili ku Seku, nafunsa nati, Samuele ndi Davide ali kuti? Ndipo wina anati, Taonani, ali ku Nayoti m'Rama. Ndipo anapita komweko ku Nayoti m'Rama; ndi mzimu wa Mulungu unamgwera iyenso; ndipo anapitirira, nanenera, mpaka anafika ku Nayoti m'Rama. Ndiponso anavula zovala zake, naneneranso pamaso pa Samuele, nagona wamaliseche usana womwe wonse, ndi usiku womwe wonse. Chifukwa chake amati, Kodi Saulonso ali pakati pa aneneri? Ndipo Davide anathawa ku Nayoti m'Rama, nadzanena pamaso pa Yonatani, Ndachitanji ine? Kuipa kwanga kuli kotani? Ndi tchimo langa la pamaso pa atate wanu ndi chiyani, kuti amafuna moyo wanga? Namyankha, Usatero iai, sudzafa; ona, atate wanga sachita kanthu kakakulu kapena kakang'ono wosandidziwitsa ine; atate wanga adzandibisiranji chinthu chimenechi? Si kutero ai. Ndipo Davide analumbiranso nati, Atate wako adziwatu kuti wandikomera mtima; nati, Yonatani asadziwe ichi, kuti angamve chisoni; koma pali Yehova, ndiponso pali moyo wako, pakati pa ine ndi imfa pali ngati phazi limodzi. Ndipo Yonatani anati kwa Davide, Chilichonse mtima wako, unena ndidzakuchitira. Nati Davide kwa Yonatani, Onani, mawa mwezi ukhala, ndipo ine ndiyenera kupita kukadya kwa mfumu, wosatsala; koma undilole ndikabisale kuthengo, kufikira tsiku lachitatu madzulo ake. Atate wako akandifuna pang'ono ponse, unene kuti, Davide anandiumirira ndimlole athamangire kwao ku Betelehemu, pakuti kumeneko kuli nsembe ya pachaka ya banja lao lonse. Tsono akati, Chabwino; kapolo wako adzakhala ndi mtendere; koma akapsa mtima, uzindikirepo kuti anatsimikiza mtima kundichitira choipa. Chifukwa chake uchitire kapolo wako zokoma mtima; popeza wamchititsa kapolo wako kupangana nawe pangano la kwa Yehova; koma ngati mwa ine muli choipa chilichonse, undiphe wekha; udzapita nane bwanji kwa atate wako? Ndipo Yonatani anati, Iai ndi pang'ono ponse; ine ndikadziwa konse kuti atate wanga anatsimikiza mtima kukuchitira choipa, sindidzadziwitsa iwe kodi? Tsono Davide anati kwa Yonatani, Adzandiuza ndani ngati atate wako alankhulira iwe mokalipa? Nati Yonatani kwa Davide, Tiyeni timuke kuthengo. Namuka onse awiri kuthengoko. Ndipo Yonatani anati kwa Davide, Yehova, Mulungu wa Israele, akhale mboni; nditaphera mwambi atate wanga mawa dzuwa lino, kapena mkucha, onani, pakakhala kanthu kabwino kakuchitira Davide, sindidzakutumiza mthenga ndi kukuululira kodi? Mulungu alange Yonatani, ndi kuonjezapo, ngati atate wanga akondwera kukuchitira choipa, ine osakuululira, ndi kukuchotsa kuti upite mumtendere; ndipo Yehova akhale nawe, monga anakhala naye atate wanga. Ndipo undionetsere chifundo cha Yehova, si pokhala ine ndi moyo pokha, kuti ndingafe; komanso usaleke kuchitira chifundo a m'nyumba yanga nthawi zonse: mungakhale m'tsogolomo Yehova atathera adani onse a Davide pa dziko lapansi. Chomwecho Yonatani anapangana pangano ndi nyumba ya Davide, ndipo Yehova anakwaniritsa izi polanga adani a Davide. Ndipo Yonatani anamlumbiritsa Davide kachiwiri, chifukwa anamkonda; popeza anamkonda monga anakonda moyo wa iye yekha. Tsono Yonatani ananena kwa Davide, Mawa mwezi ukhala; ndipo adzakufuna, popeza udzasoweka pamalo pako. Ndipo atapita masiku atatu, utsike msanga, nufike kumene unabisala tsiku la mlandu uja, nukhale pa mwala wa Ezeri. Ndipo ine ndidzaponya mivi itatu pambali pake, monga ngati ndilikuponya pachandamali. Ndipo taona, ndidzatumiza mnyamatayo, ndi kuti, Kafune miviyo. Ndikamuuza mwanayo, kuti, Taona mivi ili chakuno; uitole nubwere, popeza pali mtendere kwa iwe, palibe kanthu, pali Yehova. Koma ndikati kwa mnyamatayo, Ona mivi ili kutsogoloko; pamenepo unyamuke ulendo wako; popeza Yehova wakuuza umuke. Ndipo za chija tinakambirana iwe ndi ine, taona, Yehova ali pakati pa ife nthawi zonse. Chomwecho Davide anabisala kuthengo; ndipo pakukhala mwezi, mfumu inakhala pansi kudya. Mfumu nikhala pa mpando wake, monga ankachita nthawi zina, pa mpando wa pafupi pa khoma. Ndipo Yonatani anaimirira, ndi Abinere anakhala pa mbali ya Saulo; koma Davide anasoweka pamalo pake. Koma Saulo sananene kanthu tsiku lomwelo; chifukwa anaganizira, Kanthu kanamgwera iye, ali wodetsedwa; indedi ali wodetsedwa. Ndipo kunali tsiku lachiwiri mwezi utakhala, Davide adasowekanso pamalo pake; ndipo Saulo anati kwa Yonatani mwana wake, Mwana wa Yese walekeranji kubwera kudya dzulo ndi lero lomwe? Ndipo Yonatani anayankha Saulo, Davide anandiumiriza ndimlole amuke ku Betelehemu; nati, Ndiloleni, ndimuke; chifukwa banja lathu lipereka nsembe m'mudzimo; ndi mbale wanga anandiuzitsa ndifikeko; tsono ngati wandikomera mtima undilole ndichoke, ndikaone abale anga. Chifukwa cha ichi safika ku gome la mfumu. Pamenepo Saulo anapsa mtima ndi Yonatani, nanena naye, Iwe mwana wa mkazi wa matsutso ndi wopikisana, sindidziwa kodi kuti wasankha mwana wa Yeseyo kudzinyaza wekha, ndi usiwa wa mai wako yemwe? Popeza nthawi yonse mwana wa Yeseyo akhala ndi moyo padziko, koma sudzakhazikika iwe, kapena ufumu wako. Chifukwa chake tumiza tsopano numtengere kuno kwa ine, popeza adzafa ndithu. Ndipo Yonatani anayankha Saulo atate wake, nanena, Aphedwe chifukwa ninji? Anachitanji? Ndipo Saulo anamponyera mkondo kuti amgwaze; momwemo Yonatani anazindikira kuti atate wake anatsimikiza mtima kupha Davide. Pamenepo Yonatani anauka pagome wolunda ndithu, osadya kanthu tsiku lachiwiri la mwezi, pakuti mtima wake unali ndi chisoni chifukwa cha Davide, popeza atate wake anamchititsa manyazi. Ndipo m'mawa, Yonatani ananka kuthengoko pa nthawi imene anapangana ndi Davide, ali ndi kamnyamata. Ndipo anauza mnyamata wakeyo, Thamanga uzikatola mivi imene ndidzaponya; ndipo analikuthamanga mnyamatayu, iye anaponya muvi kuutumphitsa iye. Ndipo mnyamatayo atafika pa malo a muvi umene Yonatani anauponya, nati, Muviwo suli m'tsogolo mwako kodi? Ndipo Yonatani anafuulira mnyamatayo, nati, Yendetsa, fulumira, usaima. Ndi mnyamata wa Yonatani anatola mivi, nafika kwa mbuye wake. Koma mnyamatayo sanadziwe kanthu; Davide ndi Yonatani okha anadziwa za mlanduwo. Ndipo Yonatani anapatsa mnyamata wake zida zake, nanena naye, Muka, tenga izi kunka nazo kumudzi. Pomwepo pochoka mnyamatayo, Davide, anauka chakumwera, nagwa nkhope yake pansi, nawerama katatu; ndipo iwowa anapsompsonana, nalirirana, kufikira Davide analiritsa. Ndipo Yonatani ananena kwa Davide, Muka mumtendere, popeza tonsefe tinalumbira m'dzina la Yehova, kuti, Yehova adzakhala pakati pa ine ndi iwe, ndi pakati pa mbeu yako, nthawi zamuyaya. Ndipo iye ananyamuka nachoka; koma Yonatani anamuka kumudzi. Ndipo Davide anafika ku Nobu kwa Ahimeleki wansembeyo; ndipo Ahimeleki anadza kukomana ndi Davide alikunjenjemera, nanena naye, Muli nokha bwanji, palibe munthu wina nanu? Nati Davide kwa Ahimeleki wansembeyo, Mfumu inandilamulira ntchito, ninena nane, Asadziwe munthu aliyense kanthu za ntchito imene ndakutumira ndi kukulamulira; ndipo ndawapanga anyamatawo ku malo akuti. Chifukwa chake tsono muli ndi chiyani? Mundipatse m'dzanja langa mikate isanu, kapena chilichonse muli nacho. Ndipo wansembeyo anayankha Davide nati, Ndilibe mkate wachabe, koma ulipo mkate wopatulika; pokhapo ngati anyamatawo anadzisunga kupewa akazi. Ndipo Davide anayankha wansembeyo, nati naye, Zoonadi tinafulatira akazi monga masiku atatu; chichokere ine, zotengera za anyamatawo zinali zopatulika ungakhale unali ulendo wachabe; koposa kotani nanga zotengera zao zikhala zoyera lero? Chomwecho wansembeyo anampatsa mkate wopatulika, popeza panalibe mkate wina, koma mkate woonekera, umene adauchotsa pamaso pa Yehova, kuti akaike mkate wotentha tsiku lomwelo anachotsa winawo. Tsono munthu wina wa anyamata a Saulo anali komweko, tsiku lija, anachedwetsedwa pamaso pa Yehova; dzina lake ndiye Doegi wa ku Edomu, kapitao wa abusa a Saulo. Ndipo Davide ananena ndi Ahimeleki, Nanga pano m'dzanja mwanu mulibe mkondo kapena lupanga kodi? Chifukwa ine sindinatenge lupanga langa kapena zida zanga, popeza mlandu wa mfumu ukuti ndifulumire. Nati wansembeyo, Lupanga la Goliyati Mfilisti munamuphayo m'chigwa cha Ela, onani lilipo lokulunga m'nsalu, kumbuyo kwa efodi; mukafuna kutenga limenelo, tengani; popeza pano palibe lina. Ndipo Davide anati, Palibe lina lotere longa lijalo, ndipatseni. Ndipo Davide ananyamuka, nathawa tsiku lomwelo chifukwa cha kuopa Saulo, namuka kwa Akisi mfumu ya ku Gati. Ndipo anyamata a Akisi ananena naye, Uyu si Davide mfumu ya dzikolo kodi? Sanathirirana mang'ombe za iye kodi m'magule ao, ndi kuti, Saulo anapha zikwi zake, koma Davide zikwi zake zankhani? Ndipo Davide anasunga mau awa mumtima mwake, naopa kwambiri Akisi mfumu ya Gati. Nasanduliza makhalidwe ake pamaso pao, nadzionetsera m'manja mwao ngati wamisala, nangolembalemba pa zitseko za chipata, nakhetsa dovu lake pa ndevu yake. Tsono Akisi ananena ndi anyamata ake, Taonani, mupenya kuti munthuyo ngwa misala; mwabwera naye kwa ine chifukwa ninji? Kodi ndisowa anthu amisala kuti mwabwera ndi uyu kuti akhale wamisala pamaso panga? Kodi uyu adzalowa m'nyumba mwanga? Motero Davide anachoka kumeneko, napulumukira ku phanga la ku Adulamu; ndipo pamene abale ake ndi banja lonse la atate wake anamva, iwo anatsikira kumeneko kwa iye. Ndipo yense wosautsidwa, ndi yense wa ngongole, ndi yense wowawidwa mtima, anaunjikana kwa iye; iye nakhala mtsogoleri wao; ndipo anali nao anthu ngati mazana anai. Ndipo Davide anachoka kumeneko kunka Mizipa wa ku Mowabu; nati kwa mfumu ya Mowabu, Mulole atate wanga ndi mai wanga atuluke nakhale nanu, kufikira ndidziwa chimene Mulungu adzandichita. Ndipo anawatenga kunka nao pamaso pa mfumu ya Mowabu; ndipo iwo anakhala naye nthawi yonse Davide anali ku lingalo. Ndipo mneneri Gadi anati kwa Davide, Musamakhala m'lingamo; chokani, mulowe m'dziko la Yuda. Potero Davide anachokako, nafika ku nkhalango ya Hereti. Pakumva Saulo kuti anadziwika Davide, ndi anthu ake akukhala naye, Saulo analikukhala m'Gibea, patsinde pa mtengo wa bwemba, m'dzanja lake munali mkondo wake, ndi anyamata ake onse anaimirira pali iye. Ndipo Saulo anati kwa anyamata ake akuima chomzinga, Imvani tsopano, inu a Benjamini; kodi mwana wa Yese adzakupatsani inu nonse minda, ndi minda yamphesa, kodi adzakuikani mukhale atsogoleri a zikwi ndi a mazana; kuti inu nonse munapangana chiwembu pa ine, ndipo palibe wina wakundiululira kuti mwana wanga anapangana pangano ndi mwana wa Yese, ndipo palibe wina wa inu wakundichitira chifundo kapena kundidziwitsa kuti mwana wanga anafulumiza mnyamata wanga kundilalira monga lero lomwe? Pamenepo Doegi wa ku Edomu, anaimirira ndi anyamata a Saulo, nayankha, nati, Ine ndinamuona mwana wa Yeseyo alikufika ku Nobu, kwa Ahimeleki mwana wa Ahitubi. Ndipo iye anamfunsira kwa Yehova, nampatsa chakudya, nampatsanso lupanga la Goliyati Mfilistiyo. Pamenepo mfumu anatuma mthenga kukaitana Ahimeleki wansembeyo, mwana wa Ahitubi, ndi banja lonse la atate wake, ansembe a ku Nobu; ndipo iwo onse anafika kwa mfumu. Ndipo Saulo anati, Imva tsopano iwe mwana wa Ahitubi. Nayankha iye, Ndine, mbuye wanga. Ndipo Saulo anati kwa iye, Munapangana chiwembu pa ine bwanji, iwe ndi mwana wa Yese, kuti unampatsa iye mkate, ndi lupanga, ndi kumfunsira kwa Mulungu kuti iye andiukire, kundilalira, monga lero lomwe? Ndipo Ahimeleki anayankha mfumu, nati, Ndipo ndani mwa anyamata anu onse ali wokhulupirika ngati Davide amene, mkamwini wa mfumu; wakuyenda mu uphungu wanu, nalemekezeka m'nyumba mwanu? Kodi ndayamba lero kumfunsira kwa Mulungu? Musatero iai; mfumu asanenera mnyamata wake kanthu, kapena nyumba yonse ya atate wanga; popeza ine mnyamata wanu sindidziwa kanthu ka izi zonse, ndi pang'ono ponse. Ndipo mfumu inati, Ukufa ndithu Ahimeleki, iwe ndi banja lonse la atate wako. Mfumu niuza asilikali akuima chomzinga iye, Potolokani, iphani ansembe a Yehova; chifukwa agwirizana ndi Davide, ndipo anadziwa kuti alinkuthawa, koma sanandiululire. Koma anyamata a mfumu sanafune kutambalitsa manja ao kupha ansembe a Yehova. Pamenepo mfumu inati kwa Doegi, Potoloka iwe nuwaphe ansembewo. Ndipo Doegi wa ku Edomu anapotoloka, nagwera ansembewo, napha tsikulo makumi asanu ndi atatu mphambu asanu akuvala efodi wabafuta. Ndipo anakantha Nobu ndiwo mudzi wa ansembe ndi lupanga lakuthwa, anthu aamuna ndi aakazi, ana ndi makanda, ng'ombe ndi abulu, ndi nkhosa, ndi lupanga lakuthwa. Ndipo mmodzi wa ana a Ahimeleki, mwana wa Ahitubi, dzina lake ndiye Abiyatara, anapulumuka, nathawira kwa Davide. Ndipo Abiyatara anadziwitsa Davide kuti Saulo anapha ansembe a Yehova. Ndipo Davide anati kwa Abiyatara, Tsiku lija Doegi wa ku Edomu anali kumeneko, ndinadziwiratu kuti adzauzadi Saulo; ine ndinafetsa anthu onse a nyumba ya atate wako. Ukhale ndi ine, usaopa; popeza iye wakufuna moyo wanga afuna moyo wako; koma ndi ine udzakhala mosungika. Tsono anauza Davide, kuti, Onani Afilisti alikuponyana ndi Keila, nafunkha za m'madwale. Chifukwa chake Davide anafunsira kwa Yehova, nati, Ndimuke kodi kukakantha Afilisti aja? Ndipo Yehova anati kwa Davide, Muka, nukanthe Afilisti, ndi kupulumutsa Keila. Ndipo anyamata a Davide ananena naye, Taonani, ife tikhalira m'mantha ku Yuda kuno; koposa kotani nanga tikafika ku Keila kuponyana ndi makamu a nkhondo a Afilisti. Tsono Davide anafunsiranso kwa Yehova. Ndipo Yehova anamyankha iye, nati, Nyamuka, nutsikire ku Keila; pakuti ndidzapereka Afilisti m'dzanja lako. Chomwecho Davide ndi anthu ake anamuka ku Keila, naponyana ndi Afilisti, natenga ng'ombe zao, nawapha ndi kuwapulula kwambiri. Motero Davide analanditsa okhala m'Keila. Ndipo kunali kuti Abiyatara mwana wa Ahimeleki pakuthawira kwa Davide ku Keila, anatsika ali ndi efodi m'dzanja lake. Ndipo anthu anauza Saulo kuti Davide wafika ku Keila. Ndipo Saulo anati, Mulungu wampereka m'dzanja langa; pakuti atsekerezeka, popeza analowa m'mudzi wa zitseko ndi mipiringidzo. Ndipo Saulo anamemeza anthu onse kunkhondo, kuti atsikire ku Keila, kumangira misasa Davide ndi anthu ake. Ndipo Davide anadziwa kuti Saulo analikulingalira zomchitira zoipa; nati kwa Abiyatara wansembe, Bwera kuno ndi efodi. Nati Davide, Yehova, Mulungu wa Israele, mnyamata wanu wamva zoona kuti Saulo afuna kudza ku Keila, kuononga mudziwo chifukwa cha ine. Kodi amuna a ku Keila adzandipereka m'dzanja lake? Kodi Saulo adzatsikira ndithu, monga mnyamata wanu wamva? Yehova Mulungu wa Israele, ndikupemphani, muuze mnyamata wanu. Ndipo Yehova anati, Adzatsika. Tsono Davide anati, Kodi amuna a ku Keila adzandipereka ine ndi anyamata anga m'dzanja la Saulo? Ndipo Yehova anati, Adzakupereka. Potero Davide ndi anyamata ake, ndiwo monga ngati mazana asanu ndi limodzi, ananyamuka, natuluka ku Keila, nayendayenda kulikonse adakhoza kuyendako. Ndipo anauza Saulo kuti Davide wapulumuka ku Keila; iye naleka kumtsata. Ndipo Davide anakhala m'chipululu m'ngaka, nakhala m'dziko la mapiri m'chipululu cha Zifi. Ndipo Saulo anamfunafuna masiku onse, koma Mulungu sadampereka m'dzanja lake. Ndipo Davide anaona kuti Saulo adatuluka kudzafuna moyo wake; Davide nakhala m'chipululu cha Zifi m'nkhalango ku Horesi. Ndipo Yonatani mwana wa Saulo ananyamuka, napita kwa Davide kunkhalangoko, namlimbitsa dzanja lake mwa Mulungu. Ndipo iye ananena naye, Usaopa; chifukwa dzanja la Saulo atate wanga silidzakupeza; iwe udzakhala mfumu ya Israele, ndipo ine ndidzakhala wotsatana nawe, ichinso Saulo atate wanga achidziwa. Ndipo awiriwo anapangana pangano pamaso pa Yehova; ndipo Davide anakhala kunkhalango, koma Yonatani anapita kunyumba yake. Ndipo a ku Zifi anakwera kwa Saulo ku Gibea, nati, Davide salikubisala kwathu kodi, m'ngaka za m'nkhalango ku Horesi, m'phiri la Hakila, limene lili kumwera kwa chipululu? Chifukwa chake mfumu, tsikani, monga umo mukhumbire m'mtima mwanu kutsika; ndipo kudzakhala kwathu kumpereka iye m'dzanja la mfumu. Saulo nati, Mudalitsike inu kwa Yehova; chifukwa munandichitira ine chifundo. Mukanitu kuti mukadziwitse ndithu, ndi kudziwa ndi kuona mbuto m'mene akhalitsa, ndi amene adamuona m'menemo; chifukwa anandiuza kuti iye achita mochenjera ndithu. Chifukwa chake yang'anirani, ndi kudziwa ngaka zonse alikubisalamo iye, nimubwere kwa ine ndi mau otsimikizika, pomwepo ndidzamuka nanu; ndipo akakhala m'dzikomo, ndidzampwaira pakati pa mabanja onse a Yuda. Ndipo iwo ananyamuka, namuka ku Zifi asanapiteko Saulo; koma Davide ndi anthu ake anali ku chipululu cha Maoni, m'chigwa cha kumwera kwa chipululu. Ndipo Saulo ndi anthu ake anamuka kukamfuna. Koma wina anauza Davide; chifukwa chake anatsikira kuthanthweko, nakhala m'chipululu cha Maoni. Ndipo pamene Saulo anamva ichi, iye anamlondola Davide m'chipululu cha Maoni. Ndipo Saulo anamuka mbali ina ya phiri, Davide ndi anthu ake kuseri kwake; ndipo Davide anafulumira kuthawa, chifukwa cha kuopa Saulo; popeza Saulo ndi anthu ake anazinga Davide ndi anthu ake kwete kuti awagwire. Koma mthenga unafika kwa Saulo ndi kuti, Mufulumire kubwerera; popeza nkhondo yovumbulukira ya Afilisti yalowa m'dziko. Chomwecho Saulo anabwerera polondola Davide, nakakomana ndi Afilisti; chifukwa chake anatchula dzina lake la malo aja, Thanthwe lolekanitsa. Ndipo Davide anakwera kuchokera kumeneko, nakhala m'ngaka za Engedi. Ndipo kunali, pakubwerera Saulo potsata Afilisti, anamuuza, kuti, Taonani, Davide ali ku chipululu cha Engedi. Tsono Saulo anatenga anthu zikwi zitatu osankhika pakati pa Aisraele onse, namuka, kukafuna Davide ndi anthu ake m'matanthwe a zinkhoma. Ndipo panjira anafika ku makola a nkhosa, kumene kunali phanga; ndipo Saulo analowa kuti akadzithandize. Ndipo Davide ndi anyamata ake analikukhala m'kati mwa phangamo. Ndipo anyamata a Davide ananena naye, Onani, lero ndilo tsiku limene Yehova anati kwa inu, Onani, Ine ndidzapereka mdani wako m'dzanja lako, kuti ukamchitira iye chokukomera. Ndipo Davide ananyamuka, nadula mkawo wa mwinjiro wa Saulo mobisika. Ndipo kunali m'tsogolo mwake kuti mtima wa Davide unamtsutsa chifukwa adadula mkawo wa mwinjiro wa Saulo. Nati kwa anyamata ake, Mulungu andiletse kuchitira ichi mbuye wanga, wodzozedwa wa Yehova, kumsamulira dzanja langa, popeza iye ndiye wodzozedwa wa Yehova. Chomwecho Davide analetsa anyamata ake ndi mau awa, osawaloleza kuukira Saulo. Ndipo Saulo ananyamuka, natuluka m'phangamo, namuka njira yake. Bwino lake Davide yemwe ananyamuka, natuluka m'phangamo, nafuulira Saulo, nati, Mbuye wanga, mfumu. Ndipo pakucheuka Saulo, Davide anaweramira nkhope yake pansi, namgwadira. Davide nanena ndi Saulo, Bwanji mulikusamalira mau a anthu akuti, Onani, Davide afuna kukuchitirani choipa. Onani, lero lomwe maso anu anapenya kuti Yehova anakuperekani inu lero m'dzanja langa m'phangamo, ndipo ena anandiuza ndikupheni; koma ndinakulekani, ndi kuti, sindidzatukulira mbuye wanga dzanja langa; chifukwa iye ndiye wodzozedwa wa Yehova. Ndiponso atate wanga, penyani, inde penyani mkawo wa mwinjiro wanu m'dzanja langa; popeza ndinadula mkawo wa mwinjiro wanu, osakuphani, mudziwe, nimuone kuti mulibe choipa kapena kulakwa m'dzanja langa, ndipo sindinakuchimwirani, chinkana inu musaka moyo wanga kuti muugwire. Yehova aweruze pakati pa ine ndi inu; ndipo Yehova adzandibwezera chilango kwa inu. Monga umanena mwambi wa makolo, kuti, Uchimo utulukira mwa ochimwa; koma dzanja langa silidzakhala pa inu. Nanga mfumu ya Israele inatulukira yani; inu mulikupirikitsa yani? Galu wakufa, kapena nsabwe. Chifukwa chake Yehova akhale woweruza, naweruze pakati pa ine ndi inu, nayang'anire, nandigwirire moyo, nandipulumutse m'dzanja lanu. Ndipo kunali, pakutsiriza Davide kulankhula mau awa kwa Saulo, Saulo anati, Ndiwo mau ako kodi, mwana wanga Davide? Saulo nakweza mau ake, nalira misozi. Nati kwa Davide, Iwe ndiwe wolungama woposa ine; popeza unandibwezera zabwino, koma ine ndinakubwezera zoipa. Ndipo unatsimikiza lero lino kuti wandichitira zabwino; chifukwa sunandipha pamene Yehova anandipereka m'dzanja lako. Pakuti munthu akapeza mdani wake, adzamleka kodi kuti achoke bwino? Chifukwa chake Yehova akubwezere zabwino pa ichi unandichitira ine lero lomwe. Ndipo tsono taona ndidziwa kuti udzakhala mfumu ndithu, ndi kuti ufumu wa Israele udzakhazikika m'dzanja lako. Chifukwa chake tsono undilumbirire ndi Yehova, kuti sudzatha mbeu yanga nditamuka ine, ndi kuti sudzaononga dzina langa m'nyumba ya atate wanga. Ndipo Davide analumbirira Saulo. Saulo namuka kwao; koma Davide ndi anthu ake anakwera kunka kungaka. Ndipo Samuele anamwalira; ndi Aisraele onse anaunjikana pamodzi nalira maliro ake, namuika m'nyumba yake ku Rama. Davide ananyamuka, natsikira ku chipululu cha Parani. Ndipo panali munthu ku Maoni, amene katundu wake anali ku Karimele; iyeyu anali womveka ndithu, anali nazo nkhosa zikwi zitatu, ndi mbuzi chikwi chimodzi; ndipo analikusenga nkhosa zake ku Karimele. Tsono dzina la munthuyo ndiye Nabala, ndi dzina la mkazi wake ndiye Abigaile; ndiye mkazi wa nzeru yabwino, ndi wa nkhope yokongola; koma mwamunayo anali waphunzo ndi woipa machitidwe ake; ndipo iye anali wa banja la Kalebe. Ndipo Davide anamva kuchipululu kuti Nabala alinkusenga nkhosa zake. Davide natuma anyamata khumi, nanena kwa anyamatawo, Mukwere ku Karimele, mumuke kwa Nabala ndi kundiperekera moni; ndipo muzitero kwa wodalayo, Mtendere ukhale pa inu, mtendere ukhalenso pa nyumba yanu, ndi mtendere ukhale pa zonse muli nazo. Ndipo tsono ndamva kuti muli nao osenga nkhosa; abusa anu amene anali ndi ife, sitinawachititsa manyazi, ndipo panalibe kanthu kao kadasowa, nthawi yonse anakhala iwo ku Karimele. Mufunse anyamata anu, adzakuuzani; chifukwa chake muwakomere mtima anyamata awa, pakuti tilikufika tsiku labwino; mupatse chilichonse muli nacho m'dzanja lanu, kwa anyamata anu, ndi kwa mwana wanu Davide. Ndipo pakufika anyamata a Davide, analankhula ndi Nabala monga mau aja onse m'dzina la Davide, naleka. Koma Nabala anayankha anyamata a Davide nati, Davide ndani? Ndi mwana wa Yese ndani? Makono ano pali anyamata ambiri akungotaya ambuye ao. Kodi ndidzatenga mkate wanga, ndi madzi anga, ndi nyama imene ndinaphera osenga nkhosa anga, ndi kuzipatsa anthu amene sindidziwa kumene afumira? Chomwecho anyamata a Davide anatembenukira ku njira yao, nabwerera, nadza namuuza monga mwa mau onse awa. Ndipo Davide anati kwa anthu ake, Munthu yense wa inu amangirire lupanga lake. Namangirira munthu yense lupanga lake; ndi Davide yemwe anamangirira lupanga lake; ndipo anakwera kumtsata Davide monga anthu mazana anai, koma mazana awiri anadika akatundu. Koma mnyamata wina anauza Abigaile, mkazi wa Nabala, kuti, Onani, Davide anatumiza mithenga akuchokera kuchipululu kulonjera mbuye wathu; koma iye anawakalipira. Koma anthu aja anatichitira zabwino ndithu, sanatichititse manyazi, ndi panalibe kanthu kadatisowa, nthawi zonse tinali kuyenderana nao kubusa kuja; iwo anatikhalira ngati linga usana ndi usiku, nthawi yonse tinali nao ndi kusunga nkhosazo. Chifukwa chake tsono mudziwe ndi kulingalira chimene mudzachita; popeza anatsimikiza mtima kuchitira choipa mbuye wathu, ndi nyumba yake yonse; popeza iye ali woipa, ndipo munthu sakhoza kulankhula naye. Pomwepo Abigaile anafulumira, natenga mikate mazana awiri, ndi zikopa ziwiri za vinyo, nkhosa zisanu zoochaocha, ndi miyeso isanu ya tirigu wokazinga, ndi nchinchi za mphesa zouma zana limodzi, ndi nchinchi za nkhuyu mazana awiri, naziika pa abulu. Nati kwa anyamata ake, Nditsogolereni; onani ndidza m'mbuyo mwanu. Koma sanauze mwamuna wake Nabala. Ndipo kudatero pakuberekeka iye pa bulu wake, natsikira pa malo obisika a m'phirilo, onani, Davide ndi anthu ake analikutsikira kwa iye; iye nakomana nao. Koma Davide adanena, Zoonadi ndasunga chabe zake zonse za kaja kanali nazo m'chipululu, sikadasowa kanthu ka zake zonse; ndipo iye anandibwezera zoipa m'malo mwa zabwino. Mulungu alange adani a Davide, ndi kuonjezerapo, ngati ndisiyapo kufikira kuunika kwa m'mawa, kanthu konse ka iye, kangakhale kamwana kamphongo. Ndipo Abigaile pakuona Davide, anafulumira kutsika pa bulu, nagwa pamaso pa Davide nkhope yake pansi, namgwadira, Ndipo atagwadira pa mapazi ake anati, Pa ine, mbuye wanga, pa ine pakhale uchimowo; ndipo mulole mdzakazi wanu alankhule m'makutu anu, nimumvere mau a mdzakazi wanu. Mbuye wanga, musasamalire munthu uyu woipa, ndiye Nabala; chifukwa monga dzina lake momwemo iye; dzina lake ndiye Nabala, ndipo ali nako kupusa; koma ine mdzakazi wanu sindinaona anyamata a mbuye wanga, amene munawatumiza. Chifukwa chake tsono, mbuye wanga, pali Yehova, ndipo pali moyo wanu, popeza Yehova anakuletsani kuti mungakhetse mwazi, ndi kudzibwezera chilango ndi dzanja la inu nokha, chifukwa chake adani anu, ndi iwo akufuna kuchitira mbuye wanga choipa, akhale ngati Nabala. Ndipo mphatso iyi mdzakazi wanu ndatengera mbuye wanga, ipatsidwe kwa anyamata akutsata mbuye wanga. Mukhululukire kulakwa kwa mdzakazi wanu; pakuti Yehova adzapatsadi mbuye wanga banja lokhazikika, pakuti mbuyanga amaponya nkhondo za Yehova; ndipo mwa inu simudzapezeka choipa masiku anu onse. Ngakhale anauka anthu kukulondolani, ndi kufuna moyo wanu, koma moyo wa mbuye wanga udzamangika m'phukusi la amoyo lakukhala ndi Yehova Mulungu wanu; koma Iye adzaponya miyoyo ya adani anu kuwataya monga chotuluka m'choponyera mwala. Ndipo kudzali, pamene Yehova anachitira mbuye wanga monga mwa zabwino zonse adalankhula za inu, ndipo adadzaika inu mukhale kalonga wa Israele; mudzakhala opanda chakudodoma nacho, kapena chakusauka nacho mtima wa mbuye wanga, chakuti munakhetsa mwazi wopanda chifukwa, kapena kuti mbuye wanga anabwezera chilango ndipo Yehova akadzachitira mbuye wanga zabwino, pamenepo mukumbukire mdzakazi wanu. Ndipo Davide anati kwa Abigaile, Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israele, amene anakutumiza lero kudzandichingamira ine; ndipo, kudalitsike kuchenjera kwako, nudalitsike iwe, pakuti unandiletsa kusakhetsa mwazi, ndi kusabwezera chilango ndi dzanja la ine ndekha. Pakuti ndithu, Pali Yehova Mulungu wa Israele, amene anandiletsa lero kusapweteka iwe, ukadapanda kufulumira kubwera kundichingamira, zoonadi sindikadasiyira Nabala kufikira kutacha kanthu konse, ngakhale mwana wamwamuna mmodzi. Chomwecho Davide analandira m'dzanja lake zimene iye anamtengera; nanena naye, Ukwere kwanu mumtendere; ona, ndamvera mau ako, ndavomereza nkhope yako. Ndipo Abigaile anafika kwa Nabala; ndipo, onani, anali ndi madyerero m'nyumba mwake, monga madyerero a mfumu; ndi mtima wa Nabala unasekera kwambiri m'kati mwake, pakuti analedzera kwambiri; m'mwemo uyo sadamuuza kanthu konse, kufikira kutacha. Tsono m'mawa vinyo atamchokera Nabala, mkazi wake anamuuza zimenezi; ndipo mtima wake unamyuka m'kati mwake, iye nasanduka ngati mwala. Ndipo kunali, atapita masiku khumi, Yehova anamkantha Nabala, nafa. Ndipo pamene Davide anamva kuti Nabala adamwalira, iye anati, Alemekezedwe Yehova, amene anaweruza mlandu wa mtonzo wanga wochokera ku dzanja la Nabala, naletsa mnyamata wake pa choipa; ndipo Yehova anabwezera pamutu pa Nabala choipa chake. Ndipo Davide anatumiza wokamfunsira Abigaile, zakuti amtengere akhale mkazi wake. Ndipo anyamata a Davide pakufika kwa Abigaile ku Karimele, analankhula naye, nati, Davide anatitumiza kwa inu, kukutengani, mukhale mkazi wake. Ndipo iye ananyamuka, nawerama nkhope yake pansi, nati, Onani, mdzakazi wanu ali kapolo wakusambitsa mapazi a anyamata a mbuye wanga. Ndipo Abigaile anafulumira nanyamuka, nakwera pa bulu, pamodzi ndi anamwali ake asanu akumtsata; natsatira mithenga ya Davide, nakhala mkazi wake. Davide anatenganso Ahinowamu wa ku Yezireele, ndipo onse awiri anakhala akazi ake. Pakuti Saulo anapatsa Mikala, mwana wake, mkazi wa Davide, kwa Paliti mwana wa Laisi, wa ku Galimu. Ndipo Azifi anafika kwa Saulo ku Gibea, nati, Kodi Davide sali kubisala m'phiri la Hakila, kupenya kuchipululu! Ndipo Saulo ananyamuka, natsikira chipululu cha Zifi, ndi anthu zikwi zitatu a Israele osankhika, kukafuna Davide m'chipululu cha Zifi. Saulo namanga zithando m'phiri la Hakila kupenya kuchipululu kunjira. Koma Davide anakhala kuchipululu, naona kuti Saulo alikumfuna kuchipululu komweko. Chifukwa chake Davide anatumiza ozonda, nazindikira kuti Saulo anabwera ndithu. Ndipo Davide ananyamuka nafika pamalo paja Saulo anamangapo; ndipo Davide adaona pogona Saulo, ndi Abinere mwana wa Nere kazembe wa khamu lake; ndipo Saulo anagona pakati pa linga la magaleta, ndipo anthu adamanga zithando pomzinga pake. Pamenepo Davide anayankha nati kwa Ahimeleki Muhiti, ndi Abisa, mwana wa Zeruya, mbale wake wa Yowabu, nati, Adzatsikira nane ndani kumisasako kwa Saulo? Nati Abisai, Nditsika nanu ndine. Chomwecho Davide ndi Abisai anafika kwa anthuwo usiku; ndipo onani, Saulo anagona tulo m'kati mwa linga la magaleta, ndi mkondo wake wozika kumutu kwake; ndi Abinere ndi anthuwo anagona pomzinga iye. Ndipo Abisai anati kwa Davide, Lero Mulungu wapereka mdani wanu m'dzanja lanu; ndiloleni ndimpyoze ndi mkondo, kamodzi kokha, sindidzampyoza kawiri. Koma Davide ananena ndi Abisai, Usamuononge, ndani adzasamula dzanja lake pa wodzozedwa wa Yehova, ndi kukhala wosachimwa? Nati Davide, Pali Yehova, Yehova adzamkantha iye; kapena tsiku la imfa yake lidzafika; kapena adzatsikira kunkhondo, nadzafako. Yehova andiletse ine kusamula dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova; koma utenge mkondowo uli kumutu kwake, ndi chikho cha madzi, ndipo tiyeni, timuke. Chomwecho Davide anatenga mkondowo, ndi chikho cha madzi ku mutu wa Saulo nachoka iwowa, osawaona munthu, kapena kuzidziwa, kapena kugalamuka; pakuti onse anali m'tulo; popeza tulo tatikulu tochokera kwa Yehova tinawagwira onse. Ndipo Davide anaolokera pa phiri; pakati pao panali danga lalikulu; ndipo Davide anaitana anthuwo, ndi Abinere mwana wa Nere, nati Suyankha kodi Abinere? Tsono Abinere anayankha, nati, Ndiwe yani amene uitana mfumuyo? Davide nati kwa Abinere, Sindiwe mwamuna weniweni kodi? Ndani mwa Aisraele anafanafana ndi iwe? Unalekeranji tsono kudikira mbuye wako, mfumuyo? Pakuti anafika wina kudzaononga mfumu, mbuye wako. Ichi unachichita sichili chabwino. Pali Yehova, muyenera kufa inu, chifukwa simunadikira mbuye wanu, wodzozedwa wa Yehova. Ndipo tsono, penyani mkondo wa mfumu ndi chikho cha madzi zinali kumutu kwake zili kuti? Ndipo Saulo anazindikira mau ake a Davide, nati, Ndi mau ako awa, mwana wanga Davide? Nati Davide, Ndi mau anga mfumu, mbuye wanga. Nati iye, Chifukwa ninji mbuye wanga amalondola mnyamata wake? Pakuti ndachitanji? Kapena m'dzanja langa muli choipa chotani? Chifukwa chake mbuye wanga mfumu amvere mau a kapolo wake. Ngati ndi Yehova anakuutsirani inu kutsutsana ndi ine, alandire chopereka; koma ngati ndi ana a anthu, atembereredwe pamaso pa Yehova, pakuti anandipirikitsa lero kuti ndisalandireko cholowa cha Yehova, ndi kuti, Muka, utumikire milungu ina. Chifukwa chake tsono, mwazi wanga usagwe pansi kutali ndi Yehova; pakuti mfumu ya Israele yatuluka kudzafuna nsabwe, monga munthu wosaka nkhwali pamapiri. Pamenepo Saulo anati, Ndinachimwa; bwera, mwana wanga Davide; pakuti sindidzakuchitiranso choipa, popeza moyo wanga unali wa mtengo wapatali pamaso pako lero; ona, ndinapusa ndi kulakwa kwakukulu. Davide nayankha, nati, Tapenyani mkondo wa mfumu! Abwere mnyamata wina kuutenga. Ndipo Yehova adzabwezera munthu yense chilungamo chake ndi chikhulupiriko chake, popeza Yehova anakuperekani lero m'dzanja langa, koma sindinalola kutukulira dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova. Ndipo onani, monga lero ndinasamalira ndithu moyo wanu, momwemo usamaliridwe ndithu moyo wanga pamaso pa Yehova, ndipo Iye andipulumutse ku masautso onse. Pomwepo Saulo anati kwa Davide, Udalitsike iwe, mwana wanga Davide; udzachita ndithu champhamvu, nudzapambana. Chomwecho Davide anamuka, ndipo Saulo anabwera kwao. Ndipo Davide ananena mumtima mwake, Tsiku lina Saulo adzandipha; palibe china chondikomera koma kuti ndithawire ku dziko la Afilisti; ndipo Saulo adzakhala kakasi chifukwa cha ine, osandifunanso m'malire onse a Israele, momwemo ndidzapulumuka m'dzanja lake. Ndipo Davide ananyamuka, naoloka pamodzi ndi anthu mazana asanu ndi limodzi amene anali naye, nafika kwa Akisi mwana wa Maoki, mfumu ya ku Gati. Ndipo Davide anakhala ndi Akisi ku Gati, iye ndi anthu ake, munthu yense ndi a pabanja pake, inde Davide ndi akazi ake awiri, Ahinowamu wa ku Yezireele, ndi Abigaile wa ku Karimele, mkazi wa Nabala. Ndipo anauza Saulo kuti Davide anathawira ku Gati; ndipo iye sanamfunenso. Ndipo Davide anati kwa Akisi, Ngati mwandikomera mtima, andipatse malo kumudzi kwina kumilaga, kuti ndikakhale kumeneko; pakuti mnyamata wanu adzakhala bwanji m'mudzi wachifumu pamodzi ndi inu? Ndipo Akisi anampatsa Zikilagi tsiku lomweli; chifukwa chake Zikilagi ndi wa mafumu a Yuda kufikira lero lomwe. Ndipo kuwerenga kwake kwa masiku Davide anakhala ku dziko la Afilisti ndiko chaka chimodzi ndi miyezi inai. Ndipo Davide ndi anthu ake anakwera, nathira nkhondo yovumbulukira pa Agesuri, ndi Agerizi, ndi Aamaleke; pakuti awa ndiwo anthu akale m'dziko lija, njira ya ku Suri kufikira ku dziko la Ejipito. Ndipo Davide anapasula dzikolo, sanasunge ndi moyo mwamuna kapena wamkazi; natenga nkhosa, ndi ng'ombe, ndi abulu, ndi ngamira, ndi zovala; nabwera nafika kwa Akisi. Ndipo Akisi anati, Waponyana nkhondo ndi yani lero? Nati Davide, Ndi a kumwera kwa Ayuda, ndi a kumwera kwa Ayerameele, ndi a kumwera kwa Akeni. Ndipo Davide sadasunga wamoyo mwamuna kapena mkazi, kubwera nao ku Gati; popeza adati, Kuti angatiwulule, ndi kuti, Davide anatero, ndi makhalidwe ake ndi otere, masiku onse akukhala ku dziko la Afilisti. Ndipo Akisi anakhulupirira Davide, nati, Anadziipitsa ndithu pakati pa anthu a Israele, chifukwa chake iye adzakhala mnyamata wanga chikhalire. Ndipo kunali masiku aja, Afilisti anasonkhanitsa pamodzi makamu ao onse kunkhondo, kuti akaponyane ndi Aisraele. Ndipo Akisi ananena ndi Davide, Dziwa kuti zoonadi, udzatuluka nane ndi nkhondo, iwe ndi anthu ako. Ndipo Davide anati kwa Akisi, Potero mudzadziwe chimene mnyamata wanu adzachita. Ndipo Akisi anati kwa Davide, Chifukwa chake ndidzakuika iwe ukhale wondisungira moyo wanga masiku onse. M'menemo Samuele ndipo atafa, ndipo Aisraele onse atalira maliro ake, namuika m'Rama, m'mudzi mwao. Ndipo Saulo anachotsa m'dzikomo obwebweta onse, ndi aula onse. Ndipo Afilisti anasonkhana, nadza namanga misasa ku Sunemu; ndipo Saulo anasonkhanitsa Aisraele onse, namanga iwo ku Gilibowa. Ndipo pamene Saulo anaona khamu la Afilisti, anaopa, ndi mtima wake unanjenjemera kwakukulu. Ndipo pamene Saulo anafunsira kwa Yehova, Yehova sanamyankhe ngakhale ndi maloto, kapena ndi Urimu, kapena ndi aneneri. Tsono Saulo anati kwa anyamata ake, Mundifunire mkazi wobwebweta, kuti ndimuke kwa iye ndi kumfunsira. Ndipo anyamata ake anati kwa iye, Onani ku Endori kuli mkazi wobwebweta. Ndipo Saulo anadzizimbaitsa navala zovala zina, nanka iye pamodzi ndi anthu ena awiri, nafika kwa mkaziyo usiku; nati iye, Undilotere ndi mzimu wobwebwetawo, nundiukitsire aliyense ndidzakutchulira dzina lake. Ndipo mkaziyo ananena naye, Onani, mudziwa chimene anachita Saulo, kuti analikha m'dzikomo obwebweta onse, ndi aula; chifukwa ninji tsono mulikutchera moyo wanga msampha, kundifetsa. Ndipo Saulo anamlumbirira kwa Yehova, nati, Pali Yehova, palibe chilango chidzakugwera chifukwa cha chinthu ichi. Pomwepo mkaziyo anati, Ndikuukitsireni yani? Nati iye, Undiukitsire Samuele. Ndipo mkaziyo pakuona Samuele, anafuula ndi mau akulu; ndi mkaziyo analankhula ndi Saulo, nati, Munandinyengeranji? Popeza inu ndinu Saulo. Ndipo mfumuyo inanena naye, Usaope, kodi ulikona chiyani? Mkaziyo nanena ndi Saulo, Ndilikuona milungu ilikukwera kutuluka m'kati mwa dziko. Ndipo ananena naye, Makhalidwe ake ndi otani? Nati iye, Nkhalamba ilikukwera yovala mwinjiro. Pamenepo Saulo anazindikira kuti ndi Samuele, naweramitsa nkhope yake pansi, namgwadira. Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Wandivutiranji kundikweretsa kuno? Saulo nayankha, Ndilikusautsika kwambiri, pakuti Afilisti aponyana nkhondo ndi ine, ndipo Mulungu anandichokera, osandiyankhanso, kapena ndi aneneri, kapena ndi maloto; chifukwa chake ndakuitanani, kuti mundidziwitse chimene ndiyenera kuchita. Ndipo Samuele ananena naye, Ndipo undifunsiranji ine, popeza Yehova anakuchokera, nasandulika mdani wako? Ndipo Yehova yekha wachita monga ananena pakamwa panga; ndipo Yehova wang'amba ufumuwo, kuuchotsa m'dzanja lako, ndi kuupatsa mnansi wako, ndiye Davide. Chifukwa sunamvera mau a Yehova, ndi kukwaniritsa mkwiyo wake woopsa pa Amaleke, chifukwa chake Yehova wakuchitira chinthu ichi lero. Ndiponso Yehova adzapereka Israele pamodzi ndi iwe m'dzanja la Afilisti; ndipo mawa iwe ndi ana ako mudzakhala kuli ine; Yehova adzaperekanso khamu la Aisraele m'dzanja la Afilisti. Pomwepo Saulo anagwa pansi tantha, naopa kwakukulu, chifukwa cha mau a Samuele; ndipo analibe mphamvu; pakuti tsiku lonse ndi usiku wake wonse anakhala osadya kanthu. Ndipo mkaziyo anafika kwa Saulo, naona kuti ali wovutika kwambiri, nanena naye, Onani, mdzakazi wanu anamvera mau anu, ndipo ndinataya moyo wanga, ndi kumvera mau anu munalankhula ndi ine. Chifukwa chake tsono, mumverenso mau a mdzakazi wanu, nimundilole kuika kakudya pamaso panu; ndipo mudye, kuti mukhale ndi mphamvu pakumuka. Koma iye anakana, nati, Sindifuna kudya. Koma anyamata ake, pamodzi ndi mkaziyo anamkakamiza; iye anamvera mau ao. Chomwecho anauka pansi, nakhala pakama. Ndipo mkaziyo anali ndi mwanawang'ombe wonenepa m'nyumbamo; ndipo anafulumira, namupha, natenga ufa naukanyanga mkate wopanda chotupitsa; nabwera nazo kwa Saulo ndi kwa anyamata ake; nadya iwowa. Atatero ananyamuka, nachoka usiku womwewo. Tsono Afilisti anasonkhanitsa makamu ao onse ku Afeki; ndipo Aisraele anamanga ku chitsime cha m'Yezireele. Ndipo akalonga a Afilisti ananyamuka ndi mazana ao ndi zikwi zao; ndipo Davide ndi anthu ake ananyamuka ndi a pambuyo pamodzi ndi Akisi. Ndipo akalonga a Afilisti anati, Ahebri awa achitanji pano? Ndipo Akisi ananena kwa akalonga a Afilisti, Uyu si Davide uja mnyamata wa Saulo, mfumu ya Israele, amene wakhala nane masiku awa kapena zaka izi, ndipo sindinapeza kulakwa mwa iye, kuyambira tsiku lija anaphatikana nane kufikira lero. Koma akalonga a Afilisti anapsa naye mtima; nanena naye akalonga a Afilisti, Bwezani munthuyu, abwerere kumalo kwake kumene munamuikako, asatsikire nafe kunkhondo, kuti kunkhondoko angasanduke mdani wathu; pakuti uyu adzadziyanjanitsa ninji ndi mfumu yake? Si ndi mitu ya anthu awa? Uyu si Davide kodi amene anamthirirana mang'ombe m'magulu ao, kuti, Saulo anapha zikwi zake, koma Davide zikwi zake zankhani? Ndipo Akisi anaitana Davide, nanena naye, Pali Yehova, wakhala woongoka mtima, ndipo kutuluka kwako ndi kubwera kwako pamodzi ndi ine m'gulumo kundikomera; pakuti sindinaona choipa mwa iwe kuyambira tsiku la kufika kwako kufikira lero; koma akalongawo sakukomera mtima. Chifukwa chake, bwerera, numuke mumtendere, kuti angaipidwe mtima nawe akalonga a Afilisti. Ndipo Davide ananena ndi Akisi, Koma ndinachitanji? Ndipo munapeza chiyani mu mnyamata wanu nthawi yonse ndili pamaso panu kufikira lero, kuti sindingapite kukaponyana nkhondo ndi adani a mbuye wanga mfumu? Ndipo Akisi anayankha nanena ndi Davide, Ndidziwa kuti pamaso panga uli wabwino, ngati mthenga wa Mulungu; koma akalonga a Afilisti anena, Iye asamuke nafe kunkhondoko. Chifukwa chake ulawirire m'mawa pamodzi ndi anyamata a mbuye wako amene anabwera nawe; ndipo mutauka m'mawa, mumuke kutacha. Chomwecho Davide analawirira, iye ndi anthu ake, kuti amuke m'mawa ndi kubwera ku dziko la Afilisti. Ndipo Afilisti anakwera Yezireele. Ndipo kunali, pakufika Davide ndi anthu ake ku Zikilagi tsiku lachitatu, Aamaleke adaponya nkhondo yovumbulukira kumwera, ndi ku Zikilagi, nathyola Zikilagi nautentha ndi moto; nagwira akazi ndi onse anali m'mwemo, akulu ndi ang'ono; sanaphe mmodzi, koma anawatenga, namuka. Ndipo pamene Davide ndi anthu ake anafika kumudziko, onani, unatenthedwa ndi moto; ndi akazi ao ndi ana ao aamuna ndi aakazi anatengedwa ukapolo. Ndipo Davide ndi anthu amene anali naye anakweza mau ao, nalira misozi, kufikira analibe mphamvu yakuliranso. Ndipo akazi awiri a Davide anatengedwa ukapolo, Ahinowamu wa ku Yezireele ndi Abigaile mkazi wa Nabala wa ku Karimele. Ndipo Davide anadololoka kwambiri, pakuti anthu ananena za kumponya iye miyala, pakuti mtima wao wa anthu onse unali ndi chisoni, yense chifukwa cha ana ake aamuna ndi aakazi. Koma Davide anadzilimbikitsa mwa Yehova Mulungu wake. Ndipo Davide ananena ndi Abiyatara wansembeyo, mwana wa Ahimeleki, Unditengere kuno efodi. Abiyatara nabwera ndi efodi kwa Davide. Ndipo Davide anafunsira kwa Yehova, nati, Ndikalondola khamulo ndidzalipeza kodi? Ndipo anamyankha kuti, Londola, pakuti zoonadi udzawapeza, ndi kulanditsa zonse. Chomwecho Davide anamuka, iye ndi anthu mazana asanu ndi limodzi anali naye, nafika kukamtsinje Besori, pamenepo anatsala ena. Ndipo Davide anawalondola, iye ndi anthu mazana anai; koma anthu mazana awiri anatsala m'mbuyo, chifukwa analema, osakhoza kuoloka kamtsinje Besori. Ndipo ena anapeza Mwejipito kuthengo, nabwera naye kwa Davide, nampatsa chakudya, nadya iye; nampatsanso madzi kumwa; nampatsanso chigamphu cha nchinchi ya nkhuyu ndi nchinchi ziwiri za mphesa; ndipo atadya, moyo wake unabweranso mwa iye; pakuti adagona masiku atatu ndi usiku wao, osadya chakudya, osamwa madzi. Pamenepo Davide ananena naye, Ndiwe wa yani? Ufumira kuti? Nati iye, Ndili mnyamata wa ku Ejipito, kapolo wa Mwamaleke; mbuye wanga anandisiya, chifukwa ndinayambodwala apita masiku atatu. Tinathira nkhondo kumwera kwa Akereti ndi ku dziko lija la Ayuda, ndi kumwera kwa Kalebe; ndipo tinatentha mudzi wa Zikilagi ndi moto. Ndipo Davide ananena naye, Kodi udzanditsogolera kufikira ku khamulo? Nati iye, Mundilumbirire kwa Mulungu, kuti simudzandipha, kapena kundipereka m'dzanja la mbuye wanga, ndipo ndidzatsika nanu kuli khamu limene. Ndipo pamene anatsika naye, onani, iwo anabalalika apo ponse, analinkudya, ndi kumwa, ndi kudyerera, chifukwa cha chofunkha zambiri anazitenga ku dziko la Afilisti, ndi ku dziko la Yuda. Ndipo Davide anawakantha kuyambira madzulo kufikira usiku wa mawa wake; ndipo panalibe munthu mmodzi wa iwowa anapulumuka, koma anyamata mazana anai oberekeka pa ngamira, nathawa. Ndipo Davide analanditsa zonse anazitenga Aamaleke, napulumutsa akazi ake awiri. Ndipo sikanasoweka kanthu, kakang'ono kapena kakakulu, ana amuna kapena ana akazi, kapena chuma kapena china chilichonse cha zija anazitenga iwowa; Davide anabwera nazo zonse. Ndipo Davide anatenga nkhosa zonse ndi ng'ombe zonse, zimene anazipirikitsa patsogolo pa zoweta zaozao, nati, Izi ndi zofunkha za Davide. Ndipo Davide anafika kuli anthu mazana awiri amene analema osakhoza kutsata Davide, amenenso anawakhalitsa kukamtsinje Besori; ndipo iwowa anatuluka kuchingamira Davide, ndi amene anali naye; ndipo pakuyandikira Davide anawafunsa ngati ali bwanji. Pamenepo anthu oipa onse, ndi opanda pake a iwo amene anapita ndi Davide anayankha nati, Popeza sadamuka nafe sitidzawapatsa kanthu ka zofunkha tidazilanditsa, koma kwa munthu yense mkazi wake ndi ana ake, kuti achoke nao namuke. Davide nati, Simudzatero, abale anga inu, ndi zimene anatipatsa ife Yehova, amene anatisunga, napereka m'dzanja lathu khamu lija linadza kumenyana nafe. Ndipo ndani adzavomerezana nanu mlandu uwu? Pakuti monga gawo lake la iye wakumuka kunkhondoko, momwemo lidzakhala gawo lake la iye wakukhala ndi akatundu, adzagawana chimodzimodzi. Ndipo kuyambira tsiku lija kufikira lero lomwe anaika ichi, chikhale lemba ndi chiweruzo pa Aisraele. Ndipo pamene Davide anafika ku Zikilagi, anatumizako za zofunkhazo kwa akulu a Yuda, ndiwo abwenzi ake, nati, Siyi mphatso yanu ya zofunkha za adani a Yehova. Anatumiza kwa iwo a ku Betele, ndi kwa iwo a ku Ramoti wa kumwera, ndi kwa iwo a ku Yatiri; ndi kwa iwo a ku Aroere, ndi kwa iwo a ku Sifimoti, ndi kwa iwo a ku Esitemowa; ndi kwa iwo a ku Rakala, ndi kwa iwo a ku m'midzi ya Ayerameele, ndi kwa iwo a m'midzi ya Akeni; ndi kwa iwo a ku Horoma, ndi kwa iwo a ku Borasani, ndi kwa iwo a ku Ataki; ndi kwa iwo a ku Hebroni, ndi kumalo konse kumene Davide ndi anthu ake ankayendayenda. Ndipo Afilisti anaponyana ndi Aisraele; Aisraele nathawa pamaso pa Afilisti, nagwa olasidwa m'phiri la Gilibowa. Ndipo Afilisti anapirikitsa, osawaleka Saulo ndi ana ake; ndipo Afilisti anapha Yonatani, ndi Abinadabu, ndi Malikisuwa, ana a Saulo. Ndipo nkhondoyo inamkulira Saulo kwambiri, oponya mivi nampeza; ndipo iye anasautsika kwakukulu chifukwa cha oponya miviyo. Tsono Saulo ananena ndi wonyamula zida zake, Solola lupanga lako, undipyoze nalo; kuti osadulidwa awa angabwere ndi kundipyoza, ndi kundiseka. Koma wonyamula zida zake anakana; chifukwa anaopa ndithu. Chifukwa chake Saulo anatenga lupanga lake naligwera. Ndipo pakuona kuti Saulo anafa, wonyamula zida zake yemwe, anagwera lupanga lake, nafera limodzi ndi iye. Chomwecho adamwalira pamodzi Saulo ndi ana ake atatu, ndi wonyamula zida zake, ndi anthu ake onse, tsiku lomwe lija. Ndipo pamene Aisraele akukhala tsidya lina la chigwa, ndi iwo akukhala tsidya la Yordani, anaona kuti Aisraele alikuthawa, ndi kuti Saulo ndi ana ake anafa, iwowa anasiya midzi yao, nathawa; ndipo Afilisti anadza nakhala m'menemo. Ndipo kunali m'mawa mwake, pakubwera Afilisti kuvula akufawo, anapeza Saulo ndi ana ake atatu ali akufa m'phiri la Gilibowa. Ndipo anadula mutu wake, natenga zida zake, natumiza m'dziko lonse la Afilisti mithenga yolalikira kunyumba ya milungu yao, ndi kwa anthu. Ndipo anaika zida zake m'nyumba ya Asitaroti; napachika mtembo wake ku linga la ku Beteseani. Koma pamene a ku Yabesi-Giliyadi anamva zimene Afilisti anamchitira Saulo, ngwazi zonse zinanyamuka ndi kuchezera usiku kuyenda, natenga mtembo wa Saulo, ndi mitembo ya ana ake, pa linga la Beteseani; nafika ku Yabesi-Giliyadi naitentha kumeneko. Natenga mafupa ao nawaika patsinde pa mtengo wa bwemba uli m'Yabesi, nasala kudya masiku asanu ndi awiri. Ndipo kunali atamwalira Saulo, pamene Davide anabwera atawapha Aamaleke, ndipo Davide atakhala ku Zikilagi masiku awiri; pa tsiku lachitatu, onani, munthu anatuluka ku zithando za Saulo, ali ndi zovala zake zong'ambika, ndi dothi pamutu pake; ndipo kunatero kuti iye, pofika kwa Davide, anagwa pansi namgwadira. Ndipo Davide ananena naye, Ufumira kuti iwe? Iye nanena naye, Ndapulumuka ku zithando za Israele. Ndipo Davide ananena naye, Kunaonekanji? Undiuze. Nayankha iye, Anthu anathawa kunkhondo, ndipo ambiri anagwa nafa; ndipo Saulo ndi Yonatani mwana wake anafanso. Ndipo Davide ananena ndi mnyamata wakumuuza, Udziwa bwanji kuti Saulo ndi Yonatani mwana wake anafa? Mnyamata wakumuuzayo nati, Pamene ndinangoyenda pa phiri la Gilibowa, ndinaona, Saulo alikuyedzamira nthungo yake, ndi magaleta ndi apakavalo anamyandikiza. Ndipo iye pakucheukira m'mbuyo mwake anandiona, nandiitana. Ndipo ndinayankha, Ndine. Nanena, Ndiwe yani? Ndipo ndinayankha kuti, Ndine Mwamaleke. Ndipo anati kwa ine, Uime pa ine nundiphe, chifukwa kuwawa mtima kwandigwera ine, popeza ndikali moyobe. M'mwemo ndinakhala pambali pake ndi kumtsiriza chifukwa ndinadziwa kuti sangakhalenso ndi moyo wake, atagwa. Ndipo ndinatenga korona wa pamutu pake, ndi chigwinjiri cha pa mkono wake, ndabwera nazo kuno kwa mbuye wanga. Pomwepo Davide anagwira zovala zake nazing'amba; nateronso anthu onse okhala naye. Nabuma, nalira misozi, nasala kudya kufikira madzulo, chifukwa cha Saulo ndi mwana wake Yonatani, ndi anthu a Yehova, ndi banja la Israele, chifukwa adagwa ndi lupanga. Ndipo Davide ananena ndi mnyamata wakumuuzayo, Kwanu nkuti? Nayankha, Ine ndine mwana wa mlendo, Mwamaleke. Ndipo Davide ananena naye, Bwanji sunaopa kusamula dzanja lako kuononga wodzozedwa wa Yehova? Davide naitana wina wa anyamatawo, nati, Sendera numkanthe. Ndipo anamkantha, nafa iye. Koma asanafe, Davide adanena naye, Wadziphetsa ndi mtima wako; chifukwa pakamwa pako padachita umboni wakukutsutsa ndi kuti, Ine ndinapha wodzozedwa wa Yehova. Ndipo Davide analirira Saulo ndi Yonatani mwana wake ndi nyimbo iyi ya maliro; nawauza aphunzitse ana Ayuda nyimbo iyi ya Uta, onani inalembedwa m'buku la Yasara, Ulemerero wako, Israele, unaphedwa pa misanje yako. Ha! Adagwa amphamvu! Usachinene ku Gati, usachibukitse m'makwalala a Asikeloni, kuti ana akazi a Afilisti angasekere, kuti ana akazi a osadulidwawo angafuule mokondwera. Mapiri inu a Gilibowa, pa inu pasakhale mame kapena mvula, kapena minda yakutengako zopereka. Pakuti kumeneko zikopa za amphamvu zinatayika koipa, chikopa cha Saulo, monga cha wosadzozedwa ndi mafuta. Uta wa Yonatani sunabwerera, ndipo lupanga la Saulo silinabwerera chabe, pa mwazi wa ophedwa, pa mafuta a amphamvuwo. Saulo ndi Yonatani anali okoma ndi okondweretsa m'miyoyo yao, ndipo m'imfa yao sanasiyane; anali nalo liwiro loposa chiombankhanga, anali amphamvu koposa mikango. Ana akazi inu a Israele, mulirire Saulo, amene anakuvekani ndi zofiira zokometsetsa, amene anaika zokometsetsa zagolide pa zovala zanu. Ha! Amphamvuwo anagwa pakati pa nkhondo! Yonatani anaphedwa pamisanje pako. Ndipsinjika mtima chifukwa cha iwe, mbale wanga Yonatani; wandikomera kwambiri; chikondi chako, ndinadabwa nacho, chinaposa chikondi cha anthu akazi. Ha! Amphamvuwo anagwa, ndi zida za nkhondo zinaonengeka. Ndipo zitatha izi Davide anafunsira kwa Yehova nati, Kodi ndikwere kunka m'mudzi wina wa Yuda? Ndipo Yehova ananena naye, Kwera. Davide nanena naye, Ndikwere kuti? Ndipo anati, Ku Hebroni. Chomwecho Davide anakwera kunka kumeneko pamodzi ndi akazi ake awiri, ndiwo Ahinowamu Myezireele, ndi Abigaile mkazi wa Nabala wa ku Karimele. Ndipo Davide anakwera nao anyamata ake okhala naye, munthu yense ndi banja lake; iwowa nakhala m'midzi ya Hebroni. Ndipo anthu Ayuda anabwera namdzoza Davide pomwepo akhale mfumu ya nyumba ya Yuda. Ndipo wina anauza Davide kuti, Anthu a ku Yabesi-Giliyadi ndiwo amene anamuika Saulo. Pamenepo Davide anatumiza mithenga kwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi, nanena nao, Mudalitsike ndi Yehova inu, popeza munachitira chokoma ichi mbuye wanu Saulo, ndi kumuika. Ndipo tsopano Yehova achitire inu chokoma ndi choonadi; inenso ndidzakubwezerani chokoma ichi, popeza munachita chinthuchi. Chifukwa chake tsono manja anu alimbike, nimuchite chamuna; pakuti Saulo mbuye wanu wafa, ndi a nyumba ya Yuda anandidzoza ndikhale mfumu yao. Koma Abinere, mwana wa Nere, kazembe wa khamu la ankhondo a Saulo anatenga Isiboseti mwana wa Saulo, namuolotsa nanka naye ku Mahanaimu; namlonga ufumu wa pa Giliyadi ndi Aasiriya ndi Yezireele ndi Efuremu ndi Benjamini ndi Aisraele onse. Ndipo Isiboseti mwana wa Saulo anali ndi zaka makumi anai pakuyamba iye kukhala mfumu ya Israele, nachita ufumu zaka ziwiri. Koma a nyumba ya Yuda anatsata Davide. Ndipo Davide anali mfumu ya nyumba ya Yuda ku Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri kudza miyezi isanu ndi umodzi. Ndipo Abinere mwana wa Nere ndi anyamata a Isiboseti mwana wa Saulo anatuluka ku Mahanaimu kunka ku Gibiyoni. Ndi Yowabu mwana wa Zeruya, ndi anyamata a Davide anatuluka nakomana nao pa thamanda la Gibiyoni; nakhala pansi, ena tsidya lino, ndi ena tsidya lija la thamandalo. Ndipo Abinere ananena ndi Yowabu, Aimirire anyamata nasewere pamaso pathu. Nati Yowabu, Aimirire. Pomwepo iwo anaimirira naoloka owerengedwa, khumi ndi awiri a kwa Benjamini, ndi Isiboseti mwana wa Saulo, ndi khumi ndi awiri anyamata a Davide. Ndipo anagwirana munthu yense kugwira mutu wa mnzake, nagwaza ndi lupanga lake m'nthiti mwa mnzake. Chomwecho anagwa limodzi; chifukwa chake malo aja anatchedwa Dera la Mipeni la ku Gibiyoni. Ndipo tsikulo nkhondo inakula ndithu. Ndi Abinere ndi anthu a Israele anathawa pamaso pa anyamata a Davide. Ndipo analipo ana atatu a Zeruya, ndiwo Yowabu, Abisai ndi Asahele. Ndipo Asahele anali waliwiro ngati mbawala. Ndipo Asahele anapirikitsa Abinere. Pomwepo Abinere anacheuka nati, Kodi ndi iwe Asahele? Iye nayankha, Ndine. Ndipo Abinere ananena naye, Patuka iwe kulamanja kapena kulamanzere kwako nudzigwirire wina wa anyamatawo, nutenge zida zake. Koma Asahele anakana kupatuka pakumtsata iye. Ndipo Abinere anabwereza kunena kwa Asahele, Patuka pakunditsata ine. Ndidzakukanthiranji kukugwetsa pansi? Ndikatero ndidzaweramutsanso bwanji nkhope yanga kwa mbale wako Yowabu? Koma iye anakana kupatuka; chifukwa chake Abinere anamkantha ndi khali la mkondo m'mimba mwake, ndi khalilo linatuluka kumbuyo kwake. Ndipo anagwako, nafera pomwepo. Ndipo onse akufika kumalo kumene Asahele anagwa, namwalirapo, anaima pomwepo. Koma Yowabu ndi Abisai anampirikitsa Abinere; ndipo dzuwa linawalowera pofika ku chitunda cha Ama, chakuno cha Giya, pa njira ya ku chipululu cha Gibiyoni. Ndipo ana a Benjamini anaunjikana pamodzi kutsata Abinere, nakhala gulu limodzi, naima pamwamba pa chitunda. Pomwepo Abinere anaitana Yowabu nati, Kodi lupanga lidzaononga chionongere? Sudziwa kodi kuti kutha kwake kudzakhala udani ndithu? Tsono udzakhalanso nthawi yanji osauza anthu kubwerera pakutsata abale ao? Yowabu nati, Pali Mulungu, iwe ukadapanda kunena, anthu akadabalalika m'mawa osatsata yense mbale wake. Chomwecho Yowabu anaomba lipenga, anthu onse naima, naleka kupirikitsa Aisraele, osaponyana naonso. Ndipo Abinere ndi anthu ake anachezera usiku wonse kupyola chidikha, naoloka Yordani, napyola Bitroni lonse nafika ku Mahanaimu. Ndipo Yowabu anabwerera pakutsata Abinere. Ndipo pamene anasonkhanitsa pamodzi anthu onse anasowa anthu a Davide khumi ndi asanu ndi anai ndi Asahele. Koma anyamata a Davide anakantha anthu a Benjamini ndi a Abinere, namwalira mazana atatu mphambu makumi asanu ndi limodzi. Ndipo ananyamula Asahele namuika m'manda a atate wake ali ku Betelehemu. Ndipo Yowabu ndi anthu ake anachezera kuyenda usiku wonse, ndipo kudawachera ku Hebroni. Ndipo panali nkhondo nthawi yaitali pakati pa nyumba ya Saulo ndi nyumba ya Davide. Koma Davide analimba chilimbire, ndi nyumba ya Saulo inafooka chifokere. Ndipo ana a Davide anabadwira ku Hebroni. Mwana woyamba ndiye Aminoni, wa Ahinowamu wa ku Yezireele; wachiwiri Kiliyabu, wa Abigaile mkazi wa Nabala wa ku Karimele; ndi wachitatu Abisalomu mwana wa Maaka mwana wamkazi wa Talimai mfumu ya ku Gesuri; ndi wachinai Adoniya mwana wa Hagiti; ndi wachisanu Sefatiya mwana wa Abitala; ndi wachisanu ndi chimodzi Itireamu wa Egila mkazi wa Davide. Awa anambadwira Davide ku Hebroni. Ndipo panali, pokhala nkhondo pakati pa nyumba ya Saulo ndi nyumba ya Davide, Abinere analimbikira nyumba ya Saulo. Ndipo Saulo adali ndi mkazi wamng'ono, dzina lake ndiye Rizipa, mwana wa Aya. Ndipo Isiboseti anati kwa Abinere, Unalowana bwanji ndi mkazi wamng'ono wa atate wanga? Pomwepo Abinere anapsa mtima kwambiri pa mau a Isiboseti, nati, Ndine mutu wa galu wa Yuda kodi? Lero lino ndilikuchitira zokoma nyumba ya Saulo atate wanu, ndi abale ake, ndi abwenzi ake, ndipo sindinakuperekani m'dzanja la Davide, koma mundinenera lero lino za kulakwa naye mkazi uyu. Mulungu alange Abinere, naonjezepo, ndikapanda kumchitira Davide monga Yehova anamlumbirira; kuchotsa ufumu kunyumba ya Saulo ndi kukhazika mpando wachifumu wa Davide pa Israele ndi pa Yuda, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba. Ndipo iye sanakhoze kuyankha Abinere mau amodzi chifukwa cha kumuopa iye. Ndipo Abinere anatuma mithenga imnenere kwa Davide, nati, Dziko nla yani? Natinso, Mupangane nane pangano lanu, ndipo onani, ndidzagwirizana nanu ndi kukopa Aisraele onse atsate inu. Nati iye, Chabwino, ndidzapangana nawe; koma ndikuikira chinthu chimodzi, ndicho kuti, sudzaona nkhope yanga, koma utsogole wabwera naye Mikala mwana wamkazi wa Saulo, pamene ubwera kudzaona nkhope yanga. Ndipo Davide anatumiza mithenga kwa Isiboseti mwana wa Saulo, nati, Undipatse mkazi wanga Mikala amene ndinadzitomera ndi nsonga za makungu za Afilisti zana limodzi. Pomwepo Isiboseti anatumiza namchotsera kwa mwamuna wake, kwa Palatiele mwana wa Laisi. Ndipo mwamuna wakeyo anapita naye, nanka nalira, namtsata kufikira ku Bahurimu. Pomwepo Abinere ananena naye, Choka, bwerera; ndipo anabwerera. Ndipo Abinere analankhula nao akulu a Israele nanena nao, Inu munayamba kale kufuna Davide akhale mfumu yanu; chitani tsono, popeza Yehova analankhula za Davide, kuti, Ndi dzanja la Davide mnyamata wanga ndidzapulumutsa anthu anga Aisraele ku dzanja la Afilisti, ndi ku dzanja la adani ao onse. Ndipo Abinere analankhulanso m'kumva kwa Abenjamini; Abinere anamukanso ku Hebroni kulankhula m'makutu a Davide zonse zakukomera Aisraele ndi a nyumba yonse ya Benjamini. Abinere nafika kwa Davide ku Hebroni, ali ndi anthu makumi awiri. Ndipo Davide anawakonzera Abinere ndi anthu okhala naye madyerero. Pomwepo Abinere anati kwa Davide, Ndidzanyamuka ndi kupita ndi kusonkhanitsira mfumu mbuye wanga Aisraele onse, kuti adzapangane nanu pangano, ndi kuti mukhale mfumu pa zonse mtima wanu uzikhumba. Chomwecho Davide analawirana ndi Abinere, namuka iye mumtendere. Ndipo taonani, anyamata a Davide ndi Yowabu anabwera kuchokera ku nkhondo yovumbulukira, nakhala nazo zofunkha zambiri. Koma Abinere sanali ku Hebroni kwa Davide, chifukwa adalawirana naye ndipo adamuka mumtendere. Tsono pofika Yowabu ndi khamu lonse anali nalo, ena anamfotokozera Yowabu nati, Abinere mwana wa Nere anabwera kwa mfumu, amene analawirana naye, namuka iye mumtendere. Pomwepo Yowabu anadza kwa mfumu, nati, Mwachitanji? Taonani, Abinere anadza kwa inu, chifukwa ninji tsono munalawirana naye kuti achokedi. Mumdziwa Abinere mwana wa Nere kuti anadza kuti akunyengeni, ndi kuti adziwe kutuluka kwanu ndi kulowa kwanu, ndi kuti adziwe zonse mulikuchita inu. Ndipo Yowabu anatuluka kwa Davide, natumizira Abinere mithenga, amene anambweza ku chitsime cha Sira. Koma Davide sanachidziwe. Pofikanso Abinere ku Hebroni, Yowabu anampambutsa kupita naye pakati pa chipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, chifukwa cha mwazi wa Asahele mbale wake. Ndipo pambuyo pake, pakuchimva Davide, anati, Ine ndi ufumu wanga tikhala osachimwira mwazi wa Abinere mwana wa Nere, nthawi zonse, pamaso pa Yehova; chilango chigwere pa mutu wa Yowabu ndi pa nyumba yonse ya atate wake; ndipo kusasoweke kunyumba ya Yowabu munthu wakukhala nayo nthenda yakukha, kapena wakhate, kapena woyenda ndi ndodo, kapena wakugwa ndi lupanga, kapena wakusowa chakudya. Motero Yowabu ndi Abisai mbale wake adapha Abinere, popeza iye adapha mbale wao Asahele ku Gibiyoni, kunkhondo. Ndipo Davide anati kwa Yowabu ndi kwa anthu onse okhala naye, Ng'ambani zovala zanu, ndi kudzimangira ziguduli m'chuuno, nimulire Abinere. Ndipo mfumu Davide anatsata chithatha. Ndipo anaika Abinere ku Hebroni; ndi mfumu inakweza mau ake nilira ku manda a Abinere, nalira anthu onse. Ndipo mfumu inanenera Abinere nyimbo iyi ya maliro, niti, Kodi Abinere anayenera kufa ngati chitsiru? Manja anu sanamangidwe, mapazi anu sanalongedwe m'zigologolo; monga munthu wakugwa ndi anthu oipa momwemo mudagwa inu. Ndipo anthu onse anamliranso. Ndipo anthu onse anadza kudzadyetsa Davide chakudya kukali msana; koma Davide analumbira nati, Mulungu andilange naonjezepo, ngati ndilawa mkate kapena kanthu kena, lisanalowe dzuwa. Ndipo anthu onse anachisamalira, ndipo chinawakomera; zilizonse adazichita mfumu zidakomera anthu onse. Momwemo anthu onse ndi Aisraele onse anazindikira tsiku lija kuti sikunafumira kwa mfumu kupha Abinere mwana wa Nere. Ndipo mfumu inati kwa anyamata ake, Simudziwa kodi kuti kalonga, ndi munthu womveka, wagwa lero m'Israele? Ndipo ndikali wofooka ine lero, chinkana ndinadzozedwa mfumu; ndipo amuna awa ana a Zeruya andikakalira mtima; Yehova abwezere wochita choipa monga mwa choipa chake. Ndipo pamene Isiboseti mwana wa Saulo, anamva kuti Abinere adakafera ku Hebroni, manja ake anafooka, ndi Aisraele onse anavutika. Ndipo Isiboseti, mwana wa Saulo anali nao amuna awiri, ndiwo atsogoleri a magulu; wina dzina lake Baana, ndi dzina la mnzake ndiye Rekabu, ndiwo ana a Rimoni wa ku Beeroti, wa ana a Benjamini, pakuti Beeroti womwe unawerengedwa wa Benjamini; ndi Abeeroti anathawira ku Gitaimu; kumeneko amakhalira kufikira lero lino. Ndipo Yonatani mwana wa Saulo, anali ndi mwana wamwamuna wopunduka mapazi. Iyeyu anali wa zaka zisanu muja inamveka mbiri ya Saulo ndi Yonatani yochokera ku Yezireele; ndipo mlezi wake adamnyamula nathawa; ndipo kunali pofulumira kuthawa, iye anagwa nakhala wopunduka. Dzina lake ndiye Mefiboseti. Ndipo Rekabu ndi Baana ana a Rimoni wa ku Beeroti, anamuka, nafika kunyumba ya Isiboseti potentha dzuwa popumula iye usana. Ndipo iwo analowanso kufikira m'kati mwa nyumba, monga ngati anadzatenga tirigu; namgwaza m'mimba mwake; ndi Rekabu ndi Baana mbale wake anathawa. Koma polowa iwo m'nyumbamo iye ali chigonere pakama pake m'chipindamo, anamkantha, namupha namdula mutu wake, nautenga namuka njira ya kuchidikha usiku wonse. Ndipo anabwera nao mutu wa Isiboseti kwa Davide ku Hebroni, nanena ndi mfumu, Taonani mutu wa Isiboseti mwana wa Saulo, mdani wanu amene anafuna moyo wanu; Yehova anabwezerera chilango mbuye wanga mfumu lero lino kwa Saulo ndi mbeu yake. Ndipo Davide anayankha Rekabu ndi Baana mbale wake, ana a Rimoni wa ku Beeroti, nanena nao, Pali Yehova amene anaombola moyo wanga m'masautso onse, muja munthu wina anandiuza kuti, Onani Saulo wamwalira, ndi kulingalira kuti alikubwera nao uthenga wabwino, ndinamgwira ndi kumupha ku Zikilagi, ndiyo mphotho yake ndinampatsa chifukwa cha uthenga wake. Koposa kotani nanga, pamene anthu oipa anapha munthu wolungama pa kama wake m'nyumba yakeyake, ndidzafunsira mwazi wake ku dzanja lanu tsopano, ndi kukuchotsani ku dziko lapansi? Ndipo Davide analamulira anyamata ake, iwo nawapha, nawapachika m'mbali mwa thamanda ku Hebroni atawadula manja ndi mapazi ao. Koma mutu wa Isiboseti anautenga nauika m'manda a Abinere ku Hebroni. Pomwepo mafuko onse a Israele anabwera kwa Davide ku Hebroni, nalankhula nati, Taonani, ife ndife fupa lanu ndi mnofu wanu. Masiku anapitawo, pamene Saulo anali mfumu yathu, inu ndinu amene munatsogolera Aisraele kutuluka nao ndi kubwera nao; ndipo Yehova ananena nanu, Uzidyetsa anthu anga Israele, ndi kukhala mtsogoleri wa Israele. Chomwecho akulu onse a Israele anadza kwa mfumu ku Hebroni; ndipo mfumu Davide anapangana nao pangano ku Hebroni pamaso pa Yehova; ndipo anamdzoza Davide mfumu ya Israele. Davide anali ndi zaka makumi atatu polowa iye ufumu wake, nakhala mfumu zaka makumi anai. Ku Hebroni anachita ufumu pa Yuda zaka zisanu ndi ziwiri kudza miyezi isanu ndi umodzi; ndi ku Yerusalemu anachita ufumu pa Aisraele onse ndi Ayuda omwe zaka makumi atatu mphambu zitatu. Ndipo mfumu ndi anthu ake anamuka ku Yerusalemu kuyambana nao Ayebusi, nzika za dziko; ndiwo ananena kwa Davide ndi kuti, Sudzalowa muno, koma akhungu ndi opunduka adzakupirikitsa; ndiko kunena kuti, Davide sakhoza kulowa muno. Chinkana anatero Davide anathyola linga la Ziyoni, lomwelo ndilo mudzi wa Davide. Ndipo tsiku lija Davide anati, Aliyense akakantha Ayebusi, aponye m'madzi opuwala ndi akhungu amene moyo wa Davide udana nao. Chifukwa chake akuti, Akhungu ndi opuwala sangalowe m'nyumbamo. Ndipo Davide anakhala m'linga muja, nalitcha mudzi wa Davide. Davide namanga linga pozinga ponse kuyambira ku Milo ndi m'kati momwe. Ndipo Davide anakula chikulire chifukwa Yehova Mulungu wa makamu anali naye. Ndipo Hiramu mfumu ya Tiro anatumiza mithenga kwa Davide ndi mitengo yamkungudza, ndi amisiri a matabwa, ndi omanga nyumba; iwo nammangira Davide nyumba. Ndipo Davide anazindikira kuti Yehova anamkhazikitsa mfumu ya Israele, ndi kuti anakulitsa ufumu wake chifukwa cha anthu ake Israele. Ndipo Davide anadzitengera akazi aang'ono ena ndi akazi a ulemu ena a ku Yerusalemu, atafikako kuchokera ku Hebroni; ndipo anambadwira Davide ana aamuna ndi aakazi. Maina a iwo anambadwira m'Yerusalemu ndi awa: Samuwa, ndi Sobabu, ndi Natani, ndi Solomoni, ndi Ibara ndi Elisuwa, ndi Nefegi ndi Yafiya; ndi Elisama ndi Eliyada ndi Elifeleti. Koma pamene Afilisti anamva kuti adamdzoza Davide mfumu ya Israele, Afilisti onse anakwera kukafuna Davide; ndipo Davide anachimva natsikira kungaka kuja. Tsono Afilisti anafika natanda m'chigwa cha Refaimu. Ndipo Davide anafunsira kwa Yehova nati, Kodi ndimuke kuyambana nao Afilistiwo? Mudzawapereka m'dzanja langa kodi? Ndipo Yehova ananena ndi Davide, Pita, pakuti zoonadi ndidzapereka Afilisti m'dzanja lako. Ndipo Davide anafika ku Baala-Perazimu, nawakantha kumeneko Davideyo; nati, Yehova wathyola adani anga pamaso panga ngati madzi okamulira. Chifukwa chake analitcha dzina la malowo Baala-Perazimu. Ndipo iwo anasiya kumeneko mafano ao; Davide ndi anyamata ake nawachotsa. Ndipo Afilisti anakweranso kachiwiri, natanda m'chigwa cha Refaimu. Ndipo pamene Davide anafunsira kwa Yehova, Iye anati, Usamuke, koma ukawazungulire kumbuyo kuti ukawatulukire pandunji pa mkandankhuku. Ndipo kudzali, pakumva iwe kuwayula ku nsonga za mkandankhuku, pomwepo fulumiratu, pakuti pamenepo Yehova watuluka pamaso pako kukakantha khamu la Afilisti. Ndipo Davide anatero, monga Yehova anamlamulira, nakantha Afilisti kuyambira ku Geba kufikira ku Gezere. Pambuyo pake Davide anamemezanso osankhika onse a m'Israele, anthu zikwi makumi atatu. Ndipo Davide ananyamuka, namuka nao anthu onse anali naye, nachokera ku Baale-Yuda natengako likasa la Mulungu, limene amatchula nalo Dzinalo, Dzina la Yehova wa makamu, wokhala pakati pa Akerubi. Ndipo iwo ananyamulira likasa la Mulungu pa galeta watsopano, atalitulutsa m'nyumba ya Abinadabu, ili pachitunda, ndipo Uza ndi Ahiyo ana a Abinadabu anayendetsa ng'ombe za pa galeta watsopanoyo. Potuluka nalo tsono pamodzi ndi likasa la Mulungu m'nyumba ya Abinadabu ili pachitunda, Ahiyo anatsogolera likasalo. Ndipo Davide ndi a nyumba yonse ya Israele anasewera pamaso pa Yehova, ndi zoimbira za mitundumitundu za mlombwa, ndi azeze, ndi zisakasa ndi malingaka, ndi maseche, ndi nsanje. Ndipo pofika iwo ku dwale la Nakoni, Uza anatambasula dzanja lake, nachirikiza likasa la Mulungu; chifukwa ng'ombe zikadapulumuka. Pomwepo mkwiyo wa Yehova udayaka pa Uza, ndipo Mulungu anamkantha pomwepo, chifukwa cha kusalingiriraku; nafa iye pomwepo pa likasa la Mulungu. Ndipo kudaipira Davide, chifukwa Yehova anachita chipasulo ndi Uza; natcha malowo Pereziuza, kufikira lero lino. Ndipo Davide anaopa Yehova tsiku lomwelo; nati, Ngati likasa la Yehova lidzafika kwa ine? Momwemo Davide sanafune kudzitengera likasa la Yehova lidze kumudzi wa Davide; koma Davide analipambutsira kunyumba ya Obededomu Mgiti. Ndipo likasa la Yehova linakhala m'nyumba ya Obededomu Mgiti miyezi itatu; ndipo Yehova anadalitsa Obededomu ndi banja lake lonse. Pamenepo anthu anauza mfumu Davide, kuti Yehova wadalitsa banja la Obededomu ndi zake zonse, chifukwa cha likasa la Mulungu. Chomwecho Davide anamuka nakatenga likasa la Mulungu kunyumba ya Obededomu, nakwera nalo kumudzi wa Davide, ali ndi chimwemwe. Ndipo kunali, pamene akunyamula likasa la Yehova atayenda mapazi asanu ndi limodzi, iye anapha nsembe ng'ombe ndi chonenepa china. Ndipo Davide anavina ndi mphamvu yake yonse pamaso pa Yehova; Davide nadzimangirira efodi wabafuta. Chomwecho Davide ndi a nyumba yonse ya Israele anakwera nalo likasa la Yehova, ndi chimwemwe ndi kulira kwa malipenga. Ndipo kunali pamene likasa la Yehova linafika m'mudzi wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Saulo, analikupenya pazenera, naona mfumu Davide alikuvina ndi kusewera pamaso pa Yehova, nampeputsa mumtima mwake. Ndipo pamene adalowa nalo likasa la Mulungu analiika pamalo pake pakati pa hema amene Davide adaliutsira; ndipo Davide anapereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika pamaso pa Yehova. Pamene Davide adatsiriza kupereka nsembe yopsereza ndi zoyamika, iye anawadalitsa anthuwo m'dzina la Yehova wa makamu. Ndipo anagawira anthu onse, ndiwo unyinji wonse wa Israele, amuna ndi akazi, kwa munthu yense mtanda wa mkate ndi nthuli ya nyama, ndi nchinchi ya mphesa. Ndipo anthu aja onse anabwera yense kunyumba yake. Pamenepo Davide anabwerera kudalitsa nyumba yake. Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Saulo anatulukira kwa Davide, nati; Ha! Lero mfumu ya Israele inalemekezeka ndithu, amene anavula lero pamaso pa adzakazi a anyamata ake, monga munthu woluluka avula wopanda manyazi! Koma Davide ananena ndi Mikala, Ndatero pamaso pa Yehova, amene anandisankha ine ndi kupitirira atate wako ndi banja lake lonse, nandiika ndikhale mtsogoleri wa anthu a Yehova, wa Israele, chifukwa chake ndidzasewera pamaso pa Yehova. Ndipo ndidzaonjezanso kukhala ngati munthu woluluka, ndidzakhala wodzichepetsa m'maso a ine mwini; ndipo adzakazi udanenawo, ndi amenewo ndidzalemekezedwa. Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Saulo sanaone mwana kufikira tsiku la imfa yake. Ndipo kunali pakukhala mfumuyo m'nyumba mwake, atampumulitsa Yehova pa adani ake onse omzungulira, mfumuyo inanena ndi Natani mneneriyo, Onani ndilikukhala ine m'nyumba yamikungudza, koma likasa la Mulungu lili m'kati mwa nsalu zotchinga. Ndipo Natani anati kwa mfumuyo, Mukani muchite chonse chili mumtima mwanu, pakuti Yehova ali nanu. Ndipo kunali usiku womwewo mau a Yehova anafika kwa Natani, kuti, Kauze mtumiki wanga Davide, kuti, Atero Yehova, Kodi iwe udzandimangira nyumba yakuti ndikhalemo Ine? Pakuti sindinakhala m'nyumba kuyambira tsiku lija ndinatulutsa ana a Israele ku Ejipito kufikira lero lomwe, koma ndinayenda m'chihema ndi m'nyumba wamba. M'malo monse ndinayendamo limodzi ndi ana onse a Israele kodi ndinanena ndi fuko limodzi la Aisraele, limene ndinalamulira kudyetsa anthu anga Aisraele, kuti, Munalekeranji kundimangira nyumba yamikungudza? Chifukwa chake tsono udzatero kwa mtumiki wanga Davide, Atero Yehova wa makamu, Ndinakuchotsa kubusako kumene unalikutsata nkhosa kuti udzakhale mfumu ya anthu anga, ndiwo Israele. Ndipo ndinali nawe kulikonse unamukako, ndi kuononga adani ako onse pamaso pako; ndipo ndidzamveketsa dzina lako, monga dzina la akulu ali pa dziko lapansi. Ndipo ndidzaikira anthu anga Israele malo, ndi kuwaoka kuti akakhale m'malo ao a iwo okha, osasunthikanso. Ndipo anthu a mphulupulu sadzawavutanso, monga poyamba paja, monga kuyambira tsiku lija ndinalamulira oweruza kuyang'anira anthu anga Israele; ndipo ndidzakupumulitsa kwa adani ako onse. Yehova akuuzanso kuti Yehova adzakumangira banja. Pamene masiku ako akadzakwaniridwa, ndipo iwe udzagona ndi makolo ako, Ine ndidzaukitsa mbeu yako pambuyo pako, imene idzatuluka m'matumbo mwako, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake. Iye adzamangira dzina langa nyumba, ndipo ndidzakhazikitsa chimpando cha ufumu wake ku nthawi zonse. Ndidzakhala atate wake, iye nadzakhala mwana wanga; akachita choipa ndidzamlanga ndi ndodo ya anthu, ndi mikwapulo ya ana a anthu; koma chifundo changa sichidzamchokera iye, monga ndinachichotsera Saulo amene ndinamchotsa pamaso pako. Ndipo nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhazikikadi ku nthawi zonse pamaso pako; mpando wachifumu wako udzakhazikika ku nthawi zonse. Monga mwa mau onse awa ndi monga mwa masomphenya onse awa, momwemo Natani analankhula ndi Davide. Pomwepo Davide mfumu analowa, nakhala pansi pamaso pa Yehova; nati, Ine ndine yani, Yehova Mulungu, ndi banja langa ndi chiyani kuti munandifikitsa pano? Ndipo ichinso chinali pamaso panu chinthu chaching'ono, Yehova Mulungu; koma munanenanso za banja la mnyamata wanu kufikira nthawi yaikulu ilinkudza; ndipo mwatero monga mwa machitidwe a anthu, Yehova Mulungu! Ndipo Davide adzaonjezanso kunenanso ndi Inu? Pakuti mudziwa mnyamata wanu, Yehova Mulungu. Chifukwa cha mau anu, ndi monga mwa mtima wanu, munachita ukulu wonse umene kuuzindikiritsa mnyamata wanu. Chifukwa chake wamkulu ndi Inu Yehova Mulungu, pakuti palibe wina wofanana ndi Inu, monga mwa zonse tinazimva ndi makutu athu. Ndiponso mtundu uti wa pa dziko lapansi ufanana ndi anthu anu, ndiwo Israele, amene Mulungu anakadziombolera akhale anthu ake, ndi kuti limveke dzina lake, ndi kukuchitirani zinthu zazikulu ndi kuchitira dziko lanu zoopsa, pamaso pa anthu anu, amene munadziombolera kuwatulutsa ku dziko la Ejipito mwa amitundu ndi milungu yao? Ndipo mwadzikhazikira anthu anu Aisraele, akhale anthu anu nthawi zonse, ndipo Inu Yehova munakhala Mulungu wao. Ndipo tsopano, Yehova Mulungu, mau amene munalankhula za mnyamata wanu ndi za nyumba yake, muwalimbikitse ku nthawi zonse nimuchite monga munalankhula. Ndipo dzina lanu likulitsidwe ku nthawi zonse, kuti Yehova wa makamu ndiye Mulungu wa Israele, ndi nyumba ya mnyamata wanu Davide idzakhazikika pamaso panu. Pakuti inu, Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, munawulula kwa mnyamata wanu kuti, Ndidzakumangira iwe nyumba; chifukwa chake mnyamata wanu analimbika mtima kupemphera pemphero ili kwa Inu. Ndipo tsopano, Yehova Mulungu, Inu ndinu Mulungu, ndi mau anu adzakhala oona, ndipo Inu munalonjezana ndi mnyamata wanu kumchitira chabwino ichi, chifukwa chake tsono chikukomereni kudalitsa nyumba ya mnyamata wanu kuti ikhale pamaso panu chikhalire; pakuti Inu, Yehova Mulungu, munachinena; ndipo nyumba ya mnyamata wanu idalitsike ndi dalitso lanu ku nthawi zonse. Ndipo m'tsogolo mwake Davide anakantha Afilisti, nawagonjetsa Davide nalanda mudzi wa Metege Ama m'manja mwa Afilisti. Ndipo anakantha Amowabu nawayesa ndi chingwe, nawagonetsa pansi; ndipo anawayesera zingwe ziwiri kupha, ndi chingwe chimodzi chathunthu kusunga ndi moyo. Ndipo Amowabu anakhala anthu a Davide, nabwera nayo mitulo. Davide anakanthanso Hadadezere, mwana wa Rehobu, mfumu ya ku Zoba, pomuka iye kukadzitengeranso ufumu wake ku chimtsinje cha Yufurate. Ndipo Davide anatenga apakavalo ake chikwi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri, ndi oyenda pansi zikwi makumi awiri; ndipo Davide anadula mitsita akavalo onse a magaleta, koma anasunga a iwo akufikira magaleta zana limodzi. Ndipo pakufika Aaramu a ku Damasiko kudzathandiza Hadadezere mfumu ya ku Zoba, Davide anakanthako Aaramu zikwi makumi awiri mphambu ziwiri. Pamenepo Davide anaika maboma m'Aramu wa Damasiko. Ndipo Aaramu anasanduka anthu a Davide, nabwera nayo mitulo. Ndipo Yehova anamsunga Davide kulikonse anamukako. Ndipo Davide anatenga zikopa zagolide zinali ndi anyamata a Hadadezere, nabwera nazo ku Yerusalemu. Ndipo ku Beta ndi ku Berotai midzi ya Hadadezere, mfumu Davide anatenga mikuwa yambiri ndithu. Ndipo pamene Toi mfumu ya ku Hamati anamva kuti Davide adakantha khamu lonse la Hadadezere, Toi anatumiza mwana wake Yoramu kwa mfumu Davide, kuti akamlonjere ndi kumdalitsa, popeza anamenyana ndi Hadadezere ndi kumkantha; pakuti pakati pa Hadadezere ndi Toi panali nkhondo. Ndipo Yoramu anabwera ndi zotengera zasiliva, ndi zotengera zagolide, ndi zotengera zamkuwa. Izi zomwe mfumu Davide anazipatula zikhale za Yehova, pamodzi ndi siliva ndi golide anapatulako za amitundu onse adawagonjetsa; za Aaramu, za Amowabu, za ana a Amoni, za Afilisti, za Amaleke, ndi zofunkha za Hadadezere, mwana wa Rehobu mfumu ya ku Zoba. Ndipo Davide anamveketsa dzina lake pamene anabwera uko adakantha Aaramu m'Chigwa cha Mchere, ndiwo anthu zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu. Ndipo anaika maboma m'Edomu; m'dziko lonse la Edomu anaika maboma, ndipo Aedomu onse anasanduka anthu a Davide. Ndipo Yehova anasunga Davide kulikonse anamukako. Ndipo Davide anakhala mfumu ya Aisraele onse, Davide naweruza ndi chilungamo milandu ya anthu onse. Ndipo Yowabu mwana wa Zeruya anayang'anira ankhondo, ndi Yehosafati mwana wa Ahiludi anali wolemba mbiri, ndi Zadoki mwana wa Ahitubi, ndi Ahimeleki mwana wa Abiyatara anali ansembe, ndi Seraya anali mlembi. Ndipo Benaya mwana wa Yehoyada anayang'anira Akereti ndi Apeleti. Ndipo ana a Davide anali ansembe ake. Ndipo Davide anati, Kodi atsalako wina wa nyumba ya Saulo, kuti ndimchitire chifundo chifukwa cha Yonatani? Ndipo panali mnyamata wa m'nyumba ya Saulo dzina lake Ziba; ndipo anamuitana iye afike kwa Davide; ndi mfumuyo inanena naye, Iwe ndiwe Ziba kodi? Nati iye, Ndine mnyamata wanu amene. Ndipo mfumu inati, Kodi atsalanso wina wa nyumba ya Saulo kuti ndimuonetsere chifundo cha Mulungu? Ziba nanena ndi mfumu, Aliponso mwana wa Yonatani wopunduka mapazi ake. Ndipo mfumu inanena naye, Ali kuti iyeyo? Ziba nanena kwa mfumu, Onani ali m'nyumba ya Makiri mwana wa Amiyele ku Lodebara. Pamenepo mfumu Davide anatumiza anthu nakatenga iye kunyumba ya Makiri mwana wa Amiyele ku Lodebara. Ndipo Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, anafika kwa Davide, nagwa nkhope yake pansi, namlambira. Ndipo Davide anati, Mefiboseti! Nayankha iye, Ndine mnyamata wanu. Ndipo Davide ananena naye, Usaopa, pakuti zoonadi ndidzakuchitira kukoma mtima chifukwa cha Yonatani atate wako; ndi minda yonse ya Saulo ndidzakubwezera, ndipo udzadya pa gome langa chikhalire. Ndipo iye anamlambira, nati, Mnyamata wanu ndani, kuti mulikupenya galu wakufa monga ine. Pomwepo mfumu inaitana Ziba, mnyamata wa Saulo, ninena naye, Za Saulo zonse ndi za nyumba yake yonse ndampatsa mwana wa mbuye wako. Ndipo uzimlimira munda wake, iwe ndi ana ako ndi anyamata ako; nuzibwera nazo zipatso zake kuti mwana wa mbuye wako akhale ndi zakudya; koma Mefiboseti, mwana wa mbuye wako, adzadya pa gome langa masiku onse. Ndipo Ziba anali nao ana amuna khumi ndi asanu, ndi anyamata makumi awiri. Pomwepo Ziba anati kwa mfumu, Monga mwa zonse mfumu mbuye wanga mulamulira mnyamata wanu, momwemo adzachita mnyamata wanu. Tsono Mefiboseti, anadya pa gome la Davide monga wina wa ana a mfumu. Ndipo Mefiboseti anali ndi mwana wamwamuna wamng'ono, dzina lake ndiye Mika. Ndipo onse akukhala m'nyumba ya Ziba anali anyamata a Mefiboseti. Chomwecho Mefiboseti anakhala ku Yerusalemu, pakuti anadya masiku onse ku gome la mfumu, ndipo anali wopunduka mapazi ake onse awiri. Ndipo kunali zitapita izi, mfumu ya ana a Amoni inamwalira, ndipo Hanuni mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake. Ndipo Davide anati, Ndidzachitira Hanuni mwana wa Nahasi zokoma, monga atate wake anandichitira ine zokoma. Chomwecho Davide anatumiza ndi dzanja la anyamata ake kuti akamsangalatse chifukwa cha atate wake. Ndipo anyamata a Davide anafika ku dziko la ana a Amoni. Koma akalonga a ana a Amoni anati kwa Hanuni mbuye wao, Kodi muganiza kuti Davide alemekeza atate wanu, popeza anakutumizirani osangalatsa? Kodi Davide sanatumize anyamata ake kwa inu, kuti ayang'ane mudziwo ndi kuuzonda ndi kuupasula? Chomwecho Hanuni anatenga anyamata a Davide nawameta ndevu zao mbali imodzi, nadula zovala zao pakati, kufikira m'matako ao, nawaleka amuke. Pamene anachiuza Davide iye anatumiza anthu kukakomana nao; pakuti amunawo anachita manyazi akulu. Niti mfumu, Bakhalani ku Yeriko kufikira zamera ndevu zanu; zitamera mubwere. Ndipo pamene ana a Amoni anazindikira kuti anadzinunkhitsa kwa Davide, ana a Amoniwo anatumiza nadzilembera Aaramu a ku Beterehobu, ndi Aaramu a ku Zoba, oyenda pansi zikwi makumi awiri, ndi mfumu ya ku Maaka ndi anthu chikwi chimodzi, ndi anthu a mfumu ya ku Tobu zikwi khumi ndi ziwiri. Ndipo pamene Davide anachimva, anatumiza Yowabu ndi khamu lonse la anthu amphamvu. Ndipo ana a Amoni anatuluka, nandandalitsa nkhondo polowera kuchipata. Ndipo Aaramu a ku Zoba ndi a ku Rehobu, ndi anthu a Tobu ndi Maaka, anali pa okha kuthengo. Ndipo pamene Yowabu anaona kuti nkhondo inamdzera kumaso ndi kumbuyo, iye anasankha amuna osankhidwa onse a Israele, nawandandalitsa cha kwa Aramu. Koma anthu otsalawo anawapereka kwa Abisai mbale wake, amene anawandandalitsa cha kwa Amoni. Ndipo iye anati, Aaramu akandipambana ine, udzandithandiza ndiwe, koma ana a Amoni akapambana iwe, tsono ndidzabwera ine kukuthandiza. Ulimbike mtima, ndipo tichite chamuna lero chifukwa cha anthu athu ndi midzi ya Mulungu wathu; Yehova nachite chomkomera. Chomwecho Yowabu ndi anthu amene anali naye anayandikira kuponyana nkhondo ndi Aaramu. Ndipo iwowa anathawa pamaso pake. Ndipo pamene ana a Amoni anaona kuti Aaramu anathawa, iwonso anathawa pamaso pa Abisai, nalowa m'mudzimo. Ndipo Yowabu anabwera kuchokera kwa ana a Amoni, nafika ku Yerusalemu. Ndipo pamene Aaramu anaona kuti Aisraele anawathyola, anasonkhana pamodzi. Ndipo Hadadezere anatumiza mthenga nakatenga Aaramu a ku tsidya la chimtsinje; iwo nafika ku Helamu, ndi Sobaki kazembe wa khamu la nkhondo la Hadadezere anawatsogolera. Ndipo wina anauza Davide; iye nasonkhanitsa Aisraele onse, naoloka Yordani nafika ku Helamu. Ndipo Aaramu anandandalitsa nkhondo yao pa Davide namenyana naye. Ndipo Aaramu anathawa pamaso pa Israele; Davide naphapo Aaramu apamagaleta mazana asanu ndi awiri, ndi apakavalo zikwi makumi anai, nakantha Sobaki kazembe wa khamu lao, nafa iye pomwepo. Ndipo pamene mafumu onse, otumikira Hadadezere, anaona kuti Aisraele anawapambana, iwo anapangana mtendere ndi Aisraele, nawatumikira. Chomwecho Aaramu anaopa kuwathandizanso ana a Amoni. Ndipo kunali pofikanso chaka, nyengo yakutuluka mafumu, Davide anatumiza Yowabu, pamodzi ndi anyamata ake, ndi Aisraele onse; ndipo iwo anasakaza ana a Amoni, naumangira misasa yankhondo Raba. Koma Davide anatsalira ku Yerusalemu. Ndipo kunali pa madzulo Davide anauka pa kama wake nayenda pa tsindwi la nyumba ya mfumu. Ndipo iye ali patsindwipo anaona mkazi alinkusamba; ndi mkaziyo anali wochititsa kaso pomuyang'ana. Ndipo Davide anatumiza munthu nafunsa za mkaziyo. Ndipo wina anati, Sindiye Bateseba, mwana wamkazi wa Eliyamu, mkazi wa Uriya Muhiti? Ndipo Davide anatumiza mithenga, namtenga iye; iye nabwera kwa iye, ndipo anagona naye, pakuti adachoka mumsambo; ndipo anabwereranso kunyumba yake. Ndipo mkaziyo anaima, natumiza munthu nauza Davide, kuti Ndili ndi pakati. Davide natumiza kwa Yowabu, nati, Unditumizire Uriya Muhiti. Ndipo Yowabu anatumiza Uriya kwa Davide. Ndipo pakufika kwa iye Uriya uja, Davide anamfunsa kuti, Yowabu ali bwanji? Ndi anthu ali bwanji? Ndi nkhondo ili bwanji? Ndipo Davide anauza Uriya, Utsikire kunyumba yako, nutsuke mapazi ako. Ndipo Uriya anachoka kunyumba ya mfumu, ndipo anamtsata munthu ndi mphatso ya mfumu. Koma Uriya anagona pa khomo la nyumba ya mfumu pamodzi ndi anyamata onse a mbuye wake, osatsikira kunyumba yake. Ndipo pamene anauza Davide kuti, Uriya sanatsikire kunyumba yake, Davide ananena ndi Uriya, Kodi sunabwera kuulendo? Chifukwa ninji sunatsikira kunyumba yako? Uriya nanena ndi Davide, Likasalo, ndi Israele, ndi Yuda, alikukhala m'misasa, ndi mbuye wanga Yowabu, ndi anyamata a mbuye wanga alikugona kuthengo, potero ndikapita ine kodi kunyumba yanga kuti ndidye, ndimwe, ndigone ndi mkazi wanga? Pali inu, pali moyo wanu, sindidzachita chinthuchi. Ndipo Davide anati kwa Uriya, Utsotse pano leronso, ndipo mawa ndidzakulola umuke. Chomwecho Uriya anakhala ku Yerusalemu tsiku lomwelo ndi m'mawa mwake. Ndipo pakumuitana Davide, iyeyo anadya namwa pamaso pake; Davide namledzeretsa; ndipo usiku anatuluka kukagona pa kama wake pamodzi ndi anyamata a mbuye wake; koma sanatsikire kunyumba yake. Ndipo m'mawa Davide analembera Yowabu kalata, wopita naye Uriya. Ndi m'kalatamo analemba kuti, Mumuike Uriya pa msongwe wa nkhondo yolimba, ndipo mumlekerere kuti akanthidwe nafe. Ndipo Yowabu atayang'anira mudziwo, anaika Uriya pomwe anadziwa kuti pali ngwazi. Ndipo akumudziwo anatuluka, namenyana ndi Yowabu; ndipo adagwapo anthu ena, ndiwo a anyamata a Davide; ndi Uriya Muhiti anafanso. Pamenepo Yowabu anatumiza munthu nauza Davide zonse za nkhondoyi; nauza mthengawo kuti, Utatsiriza kuuza mfumu zonse za nkhondozo; kudzali kuti ukapsa mtima wa mfumu nikati kwa iwe, Chifukwa ninji munayandikira pafupi potere pamudzi kukamenyana nao? Simunadziwa kodi kuti apalingawo adzaponya? Ndani anakantha Abimeleki mwana wa Yerubeseti? Sadamponyera kodi mphero mkazi wa palinga nafa iye ku Tebezi? Munasendera bwanji pafupi potere pa lingalo? Tsono udzanena, Mnyamata wanu Uriya Muhiti, iyenso adafa, Chomwecho mthengawo unamuka, nufika, nudziwitsa Davide zonse Yowabu anamtumiza. Ndipo mthengawo unati kwa Davide, Anthuwo anatilaka natulukira kwa ife kumundako, koma tinawagwera kufikira polowera kuchipata. Ndipo akuponyawo amene anali palinga anaponya anyamata anu; ndipo anyamata ena a mfumu anafa, ndi mnyamata wanu Uriya Muhiti, iyenso anafa. Pomwepo Davide ananena ndi mthengawo, Udzatero kwa Yowabu, Chisakuipire ichi, lupanga limaononga wina ndi mnzake. Onjeza kulimbitsa nkhondo yako pamudzipo, nuupasule; numlimbikitse motere. Ndipo pamene mkazi wa Uriya anamva kuti Uriya mwamuna wake adamwalira, iye analira maliro a mwamuna wake. Ndipo pakutuluka malirowo, Davide anatumiza munthu namtenga afike kwao kunyumba yake; ndipo iyeyo anakhala mkazi wake nambalira mwana wamwamuna. Koma Yehova anaipidwa ndi chinthu chimene Davide adachita. Ndipo Yehova anatumiza Natani kwa Davide. Ndipo anafika kwa iye nanena naye, Pa mudzi wina panali anthu awiri; wina wolemera, wina wosauka. Wolemerayo anali nazo zoweta zazing'ono ndi zazikulu zambiri ndithu; koma wosaukayo analibe kanthu kena koma kamwana kakakazi ka nkhosa, kamene anakagula ndi kukaweta; ndipo kameneko kanakula naye pamodzi ndi ana ake. Kanadyako chakudya chake cha iye yekha, kanamwera m'chikho cha iye yekha, kanagona pa chifukato chake, ndipo kanali kwa iye ngati mwana wake wamkazi. Ndipo kwa wolemerayo kunafika mlendo, ndipo iye analeka kutengako mwa zoweta zake zazing'ono ndi zazikulu, kuphikira mlendo amene anafika kwa iye, koma anatenga mwanawankhosa wa wosaukayo, naphikira munthu amene anafika kwa iye. Pamenepo mkwiyo wa Davide unayaka ndithu pa munthuyo, nati kwa Natani, Pali Yehova, munthu amene anachita ichi, ayenera kumupha; ndipo adzabwezera mwa mwanawankhosayo ena anai, chifukwa anachita ichi osakhala nacho chifundo. Ndipo Natani ananena kwa Davide, Munthuyo ndi inu nomwe. Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Ndinakudzoza ukhale mfumu ya Israele, ndinakupukumutsa m'dzanja la Saulo; ndinakupatsa nyumba ya mbuye wako, ndi akazi a mbuye wako pa chifukato chako, ndinakupatsanso nyumba ya Israele ndi ya Yuda; ndipo zimenezi zikadakuchepera ndikadakuonjezera zina zakutizakuti. Chifukwa ninji unapeputsa mau a Yehova ndi kuchita chimene chili choipa pamaso pake? Unakantha Uriya Muhiti ndi lupanga ndi kutenga mkazi wake akhale mkazi wako; ndipo unamupha iye ndi lupanga la ana a Amoni. Chifukwa chake tsono lupanga silidzachoka pa nyumba yako nthawi zonse, popeza unandipeputsa Ine, nudzitengera mkazi wa Uriya Muhiti akhale mkazi wako. Atero Yehova, Taona ndidzakuutsira zoipa, zobadwa m'nyumba yako ya iwe wekha; ndipo ndidzachotsa akazi ako pamaso pako ndi kuwapatsa mnansi wako, amene adzagona ndi akazi ako dzuwa lili denene. Pakuti iwe unachichita m'tseri; koma Ine ndidzachita chinthu ichi pamaso pa Aisraele onse, dzuwa lili nde. Ndipo Davide anati kwa Natani, Ndinachimwira Yehova. Natani nati kwa Davide, Ndiponso Yehova wachotsa tchimo lanu, simudzafa. Koma popeza pakuchita ichi munapatsa chifukwa chachikulu kwa adani a Yehova cha kuchitira mwano, mwanayonso wobadwira inu adzafa ndithu. Ndipo Natani anamuka kwao. Ndipo Yehova anadwaza mwana amene mkazi wa Uriya anambalira Davide, nadwala kwambiri. Chifukwa chake Davide anapempherera mwanayo kwa Mulungu; Davide nasala kudya, nalowa, nagona usiku wonse pansi. Ndipo akulu a m'nyumba yake ananyamuka, naima pa iye, kuti akamuutse pansi; koma anakana, osafuna kudya nao. Ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri mwanayo anamwalira. Ndipo anyamata a Davide anaopa kumuuza kuti mwanayo wafa, pakuti iwo anati, Onani, mwanayo akali moyo, tinalankhula naye, osamvera mau athu; tsono tidzamuuza bwanji kuti mwana wafa; sadzadzichitira choipa nanga? Koma pamene Davide anaona anyamata ake likunong'onezana, Davide anazindikira kuti mwanayo adafa; Davide nanena ndi anyamata ake, Kodi mwanayo wafa? Nati iwo, Wafa. Pamenepo Davide ananyamuka pansi, nasamba, nadzola, nasintha zovala; nafika kunyumba ya Yehova, napembedza; pamenepo anafika kunyumba yake; ndipo powauza anamuikira chakudya, nadya iye. Pamenepo anyamata ake ananena naye, Ichi mwachita nchiyani? Mwanayo akali moyo, munasala kudya ndi kumlira, koma pakufa mwanayo munyamuka ndi kudya. Nati iye, Pamene mwanayo akali ndi moyo, ndinasala kudya ndi kulira, pakuti ndinati, Adziwa ndani kapena Yehova adzandichitira chifundo kuti mwanayo akhale ndi moyo. Koma tsopano wafa, ndidzasaliranjinso kudya? Kodi ndikhoza kumbweza? Ine ndidzamuka kuli iye, koma iye sadzabweranso kwa ine. Ndipo Davide anasangalatsa Bateseba mkazi wake, nalowa kwa iye, nagona naye; ndipo anabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Solomoni. Ndipo Yehova anamkonda iye, natumiza ndi dzanja la Natani mneneriyo, namutcha dzina lake Wokondedwa ndi Yehova, chifukwa cha Yehova. Ndipo Yowabu anathira nkhondo pa Raba wa ana a Amoni, nalanda mudzi wachifumu. Yowabu natumiza mithenga kwa Davide nati, Ndaponyana ndi Raba, inde ndalanda mudzi wa pamadzi. Chifukwa chake tsono musonkhanitse anthu otsalawo, nimumangire mudziwo zithando, muulande; kuti ine ndingalande mudziwo, ndipo ungatchedwe ndi dzina langa. Ndipo Davide anasonkhanitsa anthu onse, napita ku Raba, naponyana nao, naulanda. Nachotsa korona pa mutu wa mfumu yao; kulemera kwake kunali talente wa golide; ndipo m'menemo munali miyala ya mtengo wapatali; ndipo anamuika pa mutu wa Davide. Iye natulutsa zofunkha za mudziwo zambirimbiri. Natulutsa anthu a m'mudzimo, nawacheka ndi mipeni ya manomano, ndi nkhwangwa zachitsulo; nawapsitiriza ndi chitsulo, nawapititsa m'ng'anjo yanjerwa; natero ndi midzi yonse ya ana a Amoni. Ndipo Davide ndi anthu onse anabwerera kunka ku Yerusalemu. Ndipo kunali chitapita ichi, popeza Abisalomu mwana wa Davide anali naye mlongo wake wokongola, dzina lake ndiye Tamara, Aminoni mwana wa Davide anamkonda iye. Ndipo Aminoni anapsinjikadi nayamba kudwala chifukwa cha mlongo wake Tamara, pakuti anali namwali, ndipo Aminoni anachiyesa chapatali kumchitira kanthu. Koma Aminoni anali ndi bwenzi lake, dzina lake ndiye Yonadabu, mwana wa Simea, mbale wa Davide. Ndipo Yonadabu anali munthu wochenjera ndithu. Nanena naye, Iwe mwana wa mfumu, uonderanji tsiku ndi tsiku? Sungandiuze kodi? Ndipo Aminoni anati kwa iye, Ndikonda Tamara, mlongo wa mbale wanga Abisalomu. Ndipo Yonadabu ananena naye, Ugone pa kama wako ndi kudzikokomera ulikudwala; ndipo pamene atate wako akadzakuona unene naye, Mulole mlongo wanga Tamara abwere kundipatsa kudya, nakonzere chakudyacho pamaso panga kuti ndichione ndi kuchidya cha m'manja mwake. Chomwecho Aminoni anagona, nadzikokomeza alikudwala; ndipo pamene mfumu inadza kumuona, Aminoni anati kwa mfumuyo, Mulole Tamara mlongo wanga abwere ndi kundipangira timitanda tiwiri pamaso panga, kuti ndikadye cha m'manja mwake. Ndipo Davide anatumiza mau kwao kwa Tamara, kuti, Upite kunyumba ya mlongo wako Aminoni, numkonzere chakudya. Chomwecho Tamara anapita kunyumba ya mlongo wake Aminoni; ndipo iye anali chigonere. Ndipo anatenga ufa naukanda naumba timitanda pamaso pake, nakazinga timitandato. Ndipo anatenga chiwaya natitulutsa pamaso pake; koma anakana kudya. Ndipo Aminoni anati, Anthu onse atuluke kundisiya ine. Natuluka onse, kumsiya. Ndipo Aminoni anati kwa Tamara, Bwera nacho chakudya kuchipinda kuti ndikadye cha m'manja mwako. Ndipo Tamara anatenga timitanda anatipangato, nabwera nato kuchipinda kwa Aminoni mlongo wake. Ndipo pamene anabwera nato pafupi kuti adye, iye anamgwira, nanena naye, Idza nugone nane, mlongo wanga. Koma iye anamyankha nati, Iai, mlongo wanga, usandichepetsa ine, pakuti chinthu chotere sichiyenera kuchitika m'Israele, usachita kupusa kumeneku. Ndipo ine, manyazi anga ndidzapita nao kuti? Ndipo iwenso udzakhala ngati wina wa zitsiru m'Israele. Chifukwa chake tsono ulankhule ndi mfumu; iyeyu sadzakukaniza ine. Koma iye sadafuna kumvera mau ake, ndipo popeza anali wamphamvu ndi iye, anamkakamiza, nagona naye. Atatero Aminoni anadana naye ndi chidani chachikulu kopambana; pakuti chidani chimene anamuda nacho, chinali chachikulu koposa chikondi adamkonda nacho. Ndipo Aminoni ananena naye, Nyamuka, choka. Koma iye ananena naye, Usamatero, pakuti choipa ichi chakuti ulikundipirikitsa nchachikulu choposa china chija unandichitira ine. Koma anakana kumvera. Pomwepo anaitana mnyamata wake amene anamtumikira, nati, Tulutsa mkazi uyu kwa ine, nupiringidze chitseko atapita iye. Ndipo iye anavala chovala cha mawangamawanga, popeza ana akazi a mfumu okhala anamwali amavala zotere. Ndipo mnyamata wake anamtulutsa, napiringidza chitseko atapita iye. Ndipo Tamara anathira phulusa pamutu pake, nang'amba chovala cha mawangamawanga chimene analikuvala, nagwira dzanja lake pamutu pake, namuka nayenda, nalira komveka. Ndipo Abisalomu mlongo wake ananena naye, Kodi mlongo wako Aminoni anali ndi iwe? Koma tsopano ukhale chete, mlongo wanga, iye ali mlongo wako; usavutika ndi chinthuchi. Chomwecho Tamara anakhala wounguluma m'nyumba ya Abisalomu mlongo wake. Koma pamene mfumu Davide anamva zonsezi, anakwiya ndithu. Ndipo Abisalomu sanalankhule ndi Aminoni chabwino kapena choipa, pakuti Abisalomu anamuda Aminoni popeza adachepetsa mlongo wake Tamara. Ndipo zitapita zaka ziwiri zathunthu, kunali kuti Abisalomu anali nao osenga nkhosa zake ku Baala-Hazori pafupi pa Efuremu; ndipo Abisalomu anaitana ana amuna onse a mfumu. Abisalomu nafika kwa mfumu nati, Onani, ine mnyamata wanu ndili nao osenga nkhosa; inu mfumu ndi anyamata anu mupite nane mnyamata wanu. Ndipo mfumu inati kwa Abisalomu, Iai mwana wanga, tisapite tonse, kuti tingakuchulukire. Ndipo iye anaiumirira koma inakana kupita; koma inamdalitsa. Pomwepo Abisalomu anati, Ngati nkutero, mulole mbale wanga Aminoni apite nafe. Ndipo mfumu inanena naye, Iye apitirenji nawe? Koma Abisalomu anaiumirira iyo, nilola kuti Aminoni ndi ana amuna onse a mfumu apite naye. Ndipo Abisalomu anakamulira anyamata ake, nati, Inu mukhale maso, mtima wa Aminoni ukasekera ndi vinyo, ndipo ine ndikati kwa inu, Kanthani Aminoni; pamenepo mumuphe, musaope; sindine ndakulamulirani inu mulimbike, chitani chamuna. Ndipo anyamata a Abisalomu anamchitira Aminoni monga umo Abisalomu anawalamulira. Pomwepo ana amuna onse a mfumu ananyamuka, nakwera munthu yense pa nyuru yake, nathawa. Ndipo kunali akali panjira, mau anafika kwa Davide, kuti, Abisalomu anapha ana amuna onse a mfumu, osatsalapo ndi mmodzi yense. Pamenepo mfumu inanyamuka ning'amba zovala zake nigona pansi, ndipo anyamata ake onse anaimirirapo ndi zovala zao zong'ambika. Ndipo Yonadabu mwana wa Simea mbale wa Davide anayankha nati, Mbuye wanga asaganize kuti anapha anyamata onse, ana amuna a mfumu, pakuti Aminoni yekha wafa, pakuti ichi chinatsimikizika ndi mau a Abisalomu kuyambira tsiku lija anachepetsa mlongo wake Tamara. Chifukwa chake tsono mfumu mbuye wanga asasauke mtima ndi chinthuchi, ndi kuganiza kuti ana amuna onse a mfumu afa; pakuti Aminoni yekha wafa. Koma Abisalomu anathawa. Ndipo mnyamata wakudikira anatukula maso ake nayang'ana, ndipo onani, m'mbuyo mwake anthu ambiri analikubwera m'njira yolambalala phiri. Ndipo Yonadabu ananena ndi mfumu, Onani, ana amuna a mfumu afika; monga ananena mnyamata wanu, momwemo. Ndipo kunali pakutsiriza iye kulankhula, onani, pomwepo ana amuna a mfumu anafika, nakweza mau ao, nalira misozi; ndi mfumu yomwe ndi anyamata ake analira ndi kulira kwakukulu ndithu. Koma Abisalomu anathawa, nanka kwa Talimai mwana wa Amihudi mfumu ya ku Gesuri. Ndipo Davide analira mwana wake tsiku ndi tsiku. Chomwecho anathawa Abisalomu, nanka ku Gesuri, nakakhala kumeneko zaka zitatu. Ndipo mfumu Davide analira kunka kwa Abisalomu, chifukwa anasangalatsidwa pa imfa ya Aminoni. Ndipo Yowabu mwana wa Zeruya anazindikira kuti mtima wa mfumu unalunjika kwa Abisalomu. Ndipo Yowabu anatumiza ku Tekowa, natenga kumeneko mkazi wanzeru, nanena naye, Ukokomezeke monga mfedwa, nuvale zovala za pamaliro, osadzola mafuta, koma ukhale ngati munthu wamkazi wakulira akufa nthawi yaikulu. Nulowe kwa mfumu, nulankhule nayo monga momwemo. Chomwecho Yowabu anampangira mau. Ndipo pamene mkazi wa ku Tekowayo anati alankhule ndi mfumuyo, anagwa nkhope yake pansi, namlambira, nati, Ndithandizeni mfumu. Ndipo mfumuyo inanena naye, Usowanji? Iye nayankha, Zoonadi ine ndine mkazi wamasiye, mwamuna wanga anamwalira. Ndipo mdzakazi wanu ndinali nao ana amuna awiri, ndipo awiriwo analimbana kumunda, panalibe wina wakuwaletsa, koma wina anakantha mnzake namupha. Ndipo onani, chibale chonse chinaukira mdzakazi wanu, ndi kuti, Upereke iye amene anakantha mbale wake, kuti timuphe chifukwa cha moyo wa mbale wake amene anamupha; koma pakutero adzaononga wolowa yemwe; chomwecho adzazima khala langa lotsala, ndipo sadzasiyira mwamuna wanga dzina kapena mbeu kunja kuno. Ndipo mfumu inanena ndi mkaziyo, Pita kunyumba yako, ndipo ndidzalamulira za iwe. Ndipo mkazi wa ku Tekowayo ananena ndi mfumu, Mbuye wanga mfumu, mphulupulu ikhale pa ine ndi pa nyumba ya atate wanga; ndipo mfumu ndi mpando wachifumu wao zikhale zopanda chifukwa. Ndipo mfumu inati, Ubwere naye kwa ine aliyense wakunena kanthu ndi iwe, ndipo iyeyo sadzakukhudzanso. Nati iye, Mfumu mukumbukire Yehova Mulungu wanu kuti wolipsa mwazi asaonjeze kuononga, kuti angaononge mwana wanga. Niti iyo, Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la mwana wako lidzagwa pansi. Pamenepo mkaziyo anati, Mulole mdzakazi wanu alankhule mau kwa mbuye wanga mfumu. Niti iyo Nena. Ndipo mkaziyo anati, Chifukwa ninjinso munalingalira chinthu chotere pa anthu a Mulungu? Pakuti pakulankhula mau awa mfumu ikunga wopalamula, popeza mfumu siitumiza okamtenganso woingidwa wake. Pakuti kufa tidzafa, ndipo tili ngati madzi otayika pansi amene sakhoza kuwaolanso; ngakhale Mulungu sachotsa moyo, koma alingalira njira yakuti wotayikayo asakhale womtayikira Iye. Chifukwa chake tsono chakuti ndadzanena mau awa ndi mbuye wanga mfumu, ndicho kuti anthu anandiopsa ine; ndipo mdzakazi wanu ndinati, Ndilankhuletu ndi mfumu; kapena mfumu idzachita chopempha mdzakazi wake. Pakuti mfumu idzamvera ndi kupulumutsa mdzakazi wake m'dzanja la munthu wakufuna kundiononga ine pamodzi ndi mwana wanga, kutichotsa ku cholowa cha Mulungu. Ndipo mdzakazi wanu ndinati, Mau a mbuye wanga mfumu akhale opumulitsa; mbuye wanga mfumu ali ngati mthenga wa Mulungu, kuzindikira zabwino ndi zoipa; ndipo Yehova Mulungu wanu akhale nanu. Pamenepo mfumu inayankha, ninena naye mkaziyo, Usandibisire kanthu ka zimene ndidzakufunsa iwe. Mkaziyo nati, Mbuye wanga mfumu anene. Ndipo mfumuyo inati, Kodi Yowabu adziwana ndi iwe mwa izi zonse? Mkaziyo nayankha nati, Pali moyo wanu mbuye wanga mfumu, palibe kulewa ku dzanja lamanja, kapena kulamanzere kwa zonse mudazinena mbuye wanga mfumu; pakuti mnyamata wanu Yowabu ndiye anandiuza, naika mau onse awa m'kamwa mwa mdzakazi wanu. Mnyamata wanu Yowabu anachita chinthu ichi kuti asandulize mamvekedwe a mlanduwo. Ndipo mbuye wanga ali wanzeru, monga ndi nzeru ya mthenga wa Mulungu, kudziwa zonse zili m'dziko lapansi. Ndipo mfumuyo inanena ndi Yowabu, Taonanitu, ndachita chinthu ichi; chifukwa chake, pita nubwere nayenso mnyamatayo Abisalomu. Ndipo Yowabu anagwa nkhope yake pansi, namlambira, nadalitsa mfumuyo; nati Yowabu, Lero mnyamata wanu ndadziwa kuti munandikomera mtima, mbuye wanga mfumu, popeza mfumu yachita chopempha mnyamata wake. Chomwecho Yowabu ananyamuka namka ku Gesuri, nabwera naye Abisalomu ku Yerusalemu. Ndipo mfumu inati, Apatukire kunyumba ya iye yekha, koma asaone nkhope yanga. Chomwecho Abisalomu anapatukira kunyumba ya iye yekha, wosaona nkhope ya mfumu. Ndipo m'Israele monse munalibe wina anthu anamtama kwambiri chifukwa cha kukongola kwake monga Abisalomu; kuyambira ku mapazi kufikira pakati pa mutu wake mwa iye munalibe chilema. Ndipo pometa tsitsi lake amameta potsiriza chaka, chifukwa tsitsi linamlemerera, chifukwa chake atalimeta anayesa tsitsi la pa mutu wake, napeza masekeli mazana awiri, monga mwa muyeso wa mfumu. Ndipo kwa Abisalomu kunabadwa ana amuna atatu ndi mwana wamkazi mmodzi, dzina lake ndiye Tamara, iye ndiye mkazi wokongola nkhope. Ndipo Abisalomu anakhala ku Yerusalemu zaka ziwiri zathunthu, osaona nkhope ya mfumu. Pamenepo Abisalomu anaitana Yowabu kuti akamtumize iye kwa mfumu; koma anakana kubwera kwa iye; ndipo anamuitananso nthawi yachiwiri, koma anakana kubwera. Chifukwa chake iye anati kwa anyamata ake, Onani munda wa Yowabu uli pafupi ndi wanga, ndipo iye ali ndi barele pamenepo, mukani mukamtenthere. Ndipo anyamata a Abisalomu anatentha za m'mundawo. Pamenepo Yowabu ananyamuka nafika kwa Abisalomu kunyumba yake, nanena naye, Chifukwa ninji anyamata anu anatentha za m'munda mwanga; Abisalomu nayankha Yowabu, Ona, ndinatumiza kwa iwe kuti, Bwera kuno kuti ndikutume kwa mfumu kukanena, Ine ndinabwereranji kuchokera ku Gesuri? Mwenzi nditakhala komweko; chifukwa chake tsono mundilole kuona nkhope ya mfumu; ndipo ngati mulinso mphulupulu mwa ine andiphe ndithu. Chomwecho Yowabu anadza kwa mfumu namuuza; ndipo pamene iye adaitana Abisalomu, iye anadza kwa mfumu naweramira nkhope yake pansi pamaso pa mfumu; ndipo mfumu inampsompsona Abisalomu. Ndipo kunali, chitapita ichi Abisalomu anadzikonzera galeta ndi akavalo ndi anthu makumi asanu akuthamanga momtsogolera. Ndipo Abisalomu analawirira, nakaima pa njira ya kuchipata; ndipo kunatero, pakakhala munthu aliyense ndi mlandu woyenera kufika kwa mfumu kuti aweruze, Abisalomu anamuitana, nati, Ndinu wa kumudzi uti? Ndipo anati, Mnyamata wanu ndiye wa fuko lina la Aisraele. Abisalomu nanena naye, Ona zokamba zako ndizo zabwino ndi zolungama; koma mfumu sinauze wina kuti adzamve za iwe. Abisalomu anatinso, Mwenzi atandiika ine ndikhale woweruza m'dzikomo, kuti munthu yense amene ali ndi mlandu wake kapena chifukwa chake, akadafika kwa ine; ndipo ndikadamchitira zachilungamo! Ndipo kunatero kuti pakusendera munthu aliyense kudzamlambira, iye anatambasula dzanja lake, namgwira, nampsompsona. Abisalomu anachitira zotero Aisraele onse akudza kwa mfumu kuti aweruze mlandu wao; chomwecho Abisalomu anakopa mitima ya anthu a Israele. Ndipo kunali pakutha zaka zinai Abisalomu ananena kwa mfumu, Mundilole ndimuke ku Hebroni ndikachite chowinda changa ndinachiwindira Yehova. Pakuti mnyamata wanu ndinawinda pakukhala ine ku Gesuri m'Aramu, ndi kuti, Yehova akadzandibwezeranso ndithu ku Yerusalemu, ine ndidzatumikira Yehova. Ndipo mfumu inanena naye, Muka ndi mtendere. Chomwecho ananyamuka, nanka ku Hebroni. Koma Abisalomu anatumiza ozonda ku mafuko onse a Israele, kuti, Pakumva kulira kwa lipenga, pomwepo muzinena, Abisalomu ali mfumu ku Hebroni. Ndipo pamodzi ndi Abisalomu panapita anthu mazana awiri a ku Yerusalemu ndiwo oitanidwa, namuka m'kupulukira kwao, osadziwa kanthu. Ndipo Abisalomu anaitana Ahitofele Mgiloni, mphungu wa Davide, kumudzi wake ndiwo Gilo, pamene iye analikupereka nsembe. Ndipo chiwembucho chinali cholimba; pakuti anthu anachulukachulukabe kwa Abisalomu. Ndipo mthenga unafika kwa Davide nuti, Mitima ya anthu a Israele itsata Abisalomu. Ndipo Davide ananena nao anyamata ake onse akukhala naye ku Yerusalemu, Nyamukani tithawe, tikapanda kuthawa palibe mmodzi wa ife adzapulumuka Abisalomu; fulumirani kuchoka, angatipeze msanga ndi kutigwetsera zoipa ndi kukantha mudzi ndi lupanga lakuthwa. Ndipo anyamata a mfumu ananena kwa mfumu, Onani, monga mwa zonse mbuye wathu mfumu adzasankha, anyamata anu ndife. Mfumu nituluka, ndi banja lake lonse linamtsata. Ndipo mfumu inasiya akazi khumi ndiwo akazi aang'ono, kusunga nyumbayo. Ndipo mfumu inatuluka, ndi anthu onse anamtsata; naima kunyumba ya pa yokha. Ndipo anyamata ake onse anapita naye limodzi; ndi Akereti ndi Apeleti, ndi Agiti onse, anthu mazana asanu ndi limodzi omtsata kuchokera ku Gati, anapita pamaso pa mfumu. Pomwepo mfumu inanena kwa Itai Mgiti, Bwanji ulikupita nafe iwenso? Ubwerere nukhale ndi mfumu; pakuti uli mlendo ndi wopirikitsidwa; bwerera ku malo a iwe wekha. Popeza unangofika dzulo lokha, kodi ndidzakutenga lero kuyendayenda nafe popeza ndipita pomwe ndiona popita? Ubwerere nubwereretsenso abale ako; chifundo ndi zoonadi zikhale nawe. Itai nayankha mfumu nuti, Pali Yehova, pali mbuye wanga mfumu, zoonadi apo padzakhala mbuye wanga mfumu, kapena mpa imfa kapena mpa moyo, pomwepo padzakhalanso mnyamata wanu. Ndipo Davide ananena ndi Itai, Tiye nuoloke. Ndipo Itai Mgiti anaoloka, ndi anthu ake onse, ndi ana ang'ono onse amene anali naye. Ndipo dziko lonse linalira ndi mau okweza; ndipo anthu onse anaoloka, ndi mfumu yomwe inaoloka mtsinje wa Kidroni, ndipo anthu onse anaolokera ku njira ya kuchipululu. Ndipo onani, Zadoki yemwe anadza, ndi Alevi onse pamodzi naye, alikunyamula likasa la chipangano la Mulungu; natula likasa la Mulungu; ndi Abiyatara anakwera kufikira anthu onse anatha kutuluka m'mudzimo. Ndipo mfumu inanena ndi Zadoki, Ubwerera nalo likasa la Mulungu kumudziko; akandikomera mtima Yehova, Iye adzandibwezanso, nadzandionetsanso ili, ndi pokhala pake pomwe. Koma Iye akatero kuti, Sindikondwera nawe konse; onani, ndine pano, andichitire chimene chimkomera. Ndipo mfumu inanenanso ndi Zadoki wansembeyo, Suli mlauli kodi? Ubwere kumudzi mumtendere pamodzi ndi ana ako amuna awiri, Ahimaazi mwana wako ndi Yonatani mwana wa Abiyatara. Ona ndidzaima pa madooko a m'chipululu kufikira afika mau ako akunditsimikizira ine. Chifukwa chake Zadoki ndi Abiyatara ananyamulanso likasa la Mulungu nafika nalo ku Yerusalemu. Ndipo iwo anakhala kumeneko. Ndipo Davide anakwera pa chikweza cha ku Azitona nakwera nalira misozi; ndipo anafunda mutu wake nayenda ndi mapazi osavala; ndi anthu onse amene anali naye anafunda munthu yense mutu wake ndipo anakwera, nalira misozi pokwerapo. Ndipo wina anauza Davide nati, Ahitofele ali pakati pa opangana chiwembu pamodzi ndi Abisalomu. Davide nati, Yehova, musandulize uphungu wa Ahitofele ukhale wopusa. Ndipo kunali pakufika Davide ku mutu wa phiri, kumene amapembedza Mulungu, onani, Husai Mwariki anadzakomana naye ali ndi malaya ake ong'ambika, ndi dothi pamutu pake. Ndipo Davide ananena naye, Ukapita pamodzi ndi ine udzandilemetsa; koma ukabwerera kumudzi, ndi kunena ndi Abisalomu, Ine ndine mnyamata wanu, mfumu; monga kale ndinali mnyamata wa atate wanu, momwemo tsopano ndidzakhala mnyamata wanu; pomwepo udzanditsutsira uphungu wa Ahitofele. Ndipo suli nao kumeneko Zadoki ndi Abiyatara ansembewo kodi? Motero chilichonse udzachimva cha m'nyumba ya mfumu uziuza Zadoki ndi Abiyatara ansembewo. Onani, ali nao komweko ana amuna ao awiri, Ahimaazi mwana wa Zadoki, ndi Yonatani mwana wa Abiyatara; iwowa muwatumize kuti adzandiuze chilichonse mudzachimva. Chomwecho Husai bwenzi la Davide anadza m'mudzimo; ndipo Abisalomu anafika ku Yerusalemu. Ndipo pamene Davide anapitirira pang'ono pamutu pa phiri, onani, Ziba mnyamata wa Mefiboseti anakomana naye, ali nao abulu awiri omanga mbereko, ndi pamenepo mitanda ya mikate mazana awiri, ndi nchinchi zamphesa zana limodzi, ndi zipatso za m'dzinja zana limodzi, ndi thumba la vinyo. Ndipo mfumu inanena ndi Ziba, Ulikutani ndi zimenezi? Nati Ziba, Abuluwo ndiwo kuti akaberekepo a pa banja lanu; ndi mitanda ya mikate ndi zipatso za m'dzinja ndizo zakudya za anyamata; ndi vinyoyo akufooka m'chipululu akamweko. Ndipo mfumu inati, Mwana wa mbuye wako ali kuti? Ziba nanena ndi mfumu, Onani, akhala ku Yerusalemu; pakuti anati, Lero nyumba ya Israele idzandibwezera ufumu wa atate wanga. Pomwepo mfumu inanena ndi Ziba, Ona, za Mefiboseti zonse zili zako. Ndipo Ziba anati, Ndikulambirani, mundikomere mtima, mbuye wanga mfumu. Ndipo pakufika mfumu Davide ku Bahurimu, onani, panatuluka pamenepo munthu wa banja la nyumba ya Saulo, dzina lake ndiye Simei, mwana wa Gera; iyeyu anatulukako, nayenda natukwana. Ndipo iye anaponya miyala Davide ndi anyamata onse a mfumu Davide, angakhale anthu onse ndi ngwazi zonse zinali ku dzanja lamanja ndi ku dzanja lamanzere kwake. Ndipo anatero Simei pakutukwana, Choka, choka, munthu wa mwazi iwe, woipa iwe; Yehova wabwezera pa iwe mwazi wonse wa nyumba ya Saulo, amene iwe wakhala mfumu m'malo mwake; ndipo Yehova wapereka ufumuwo m'dzanja la Abisalomu mwana wako; ndipo ona, wagwidwa m'kuipa kwako kwa iwe wekha, chifukwa uli munthu wa mwazi. Pomwepo Abisai mwana wa Zeruya ananena ndi mfumu, Galu wakufa uyu atukwaniranji mbuye wanga mfumu? Mundilole ndioloke ndi kudula mutu wake. Mfumu niti, Ndili ndi chiyani ndi inu, ana a Zeruya? Pakuti atukwana, ndi pakuti Yehova ananena naye, Utukwane Davide; ndani tsono adzanena, Watero chifukwa ninji? Ndipo Davide ananena ndi Abisai ndi anyamata ake onse, Onani, mwana wanga wotuluka m'matumbo anga, alikufuna moyo wanga; koposa kotani nanga Mbenjamini uyu? Mlekeni, atukwane, pakuti Yehova anamuuza. Kapena Yehova adzayang'anira chosayenerachi alikundichitira ine, ndipo Yehova adzandibwezera chabwino m'malo mwa kunditukwana kwa lero. Chomwecho Davide ndi anthu ake anapita m'njira, ndipo Simei analambalala paphiri popenyana naye, namuka natukwana, namponya miyala, nawaza fumbi. Ndipo mfumu ndi anthu onse amene anali naye anafika olema; ndipo iye anadzitsitsimutsa kumeneko. Ndipo Abisalomu, ndi anthu onse amuna a Israele, anafika ku Yerusalemu, ndi Ahitofele pamodzi naye. Ndipo kunali pakudza kwa Abisalomu Husai Mwariki, bwenzi la Davide, Husai ananena ndi Abisalomu, Mfumu ikhale ndi moyo. Mfumu ikhale ndi moyo. Ndipo Abisalomu ananena ndi Husai, Kodi chimenechi ndi chifundo chako cha pa bwenzi lako? Unalekeranji kupita ndi bwenzi lako? Husai nanena ndi Abisalomu, Iai; koma amene Yehova anasankha ndi anthu awa, ndi anthu onse a Israele, ine ndili wake, ndipo ndidzakhala naye iyeyu. Ndiponso ndidzatumikira yani? Si pamaso pa mwana wake nanga? Monga ndinatumikira pamaso pa atate wanu, momwemo ndidzakhala pamaso panu. Pomwepo Abisalomu ananena ndi Ahitofele, Upangire chimene ukuti tikachite. Ndipo Ahitofele ananena ndi Abisalomu, Mulowe kwa akazi aang'ono a atate wanu amene iye anawasiya kuti asunge nyumbayo; ndipo Aisraele onse adzamva kuti atate wanu aipidwa nanu; pomwepo manja a onse akukhala nanu adzalimba. Chomwecho iwo anayalira Abisalomu hema pamwamba pa nyumba; ndipo Abisalomu analowa kwa akazi aang'ono a atate wake pamaso pa Aisraele onse. Ndipo uphungu wa Ahitofele anaupangira masiku aja, unali monga ngati munthu anafunsira mau kwa Mulungu; uphungu wonse wa Ahitofele unali wotere kwa Davide ndi kwa Abisalomu. Ndipo Ahitofele ananena ndi Abisalomu, Ndiloleni ndisankhe tsopano anthu zikwi khumi ndi ziwiri, ndipo ndidzanyamuka usiku womwe uno ndi kulondola Davide; ndipo ndidzamgwera ali wolema ndi wofooka, ndi kumuopsa; ndi anthu onse amene ali naye adzathawa; pamenepo ndidzakantha mfumu yokha; ndipo anthu onsewo ndidzabwera nao kwa inu; munthu mumfunayo ali ngati onse obwerera; momwemo anthu onse adzakhala mumtendere. Ndipo mauwa anamuyenerera Abisalomu, ndi akulu onse a Israele. Pomwepo Abisalomu anati, Kaitane tsopano Husai Mwariki yemwe, timvenso chimene anene iye. Ndipo pakufika Husai kwa Abisalomu, Abisalomuyo ananena naye, Ahitofele analankhula mau akuti; tichite kodi monga mwa kunena kwake? Ngati iai, unene ndiwe. Ndipo Husai ananena ndi Abisalomu, Uphungu anaupangira lero Ahitofele suli wabwino. Husai anatinso, Mudziwa atate wanu ndi anthu ake kuti ndizo ngwazi, ndipo ali ndi mitima yowawa monga chimbalangondo chochilanda ana ake kuthengo; ndipo atate wanu ali munthu wodziwa nkhondo, sadzagona pamodzi ndi anthu. Onani, tsopanoli alikubisala kudzenje kapena kwina; ndipo kudzali poyamba kugwa ena, aliyense wakumva adzanena, Alikuphedwa anthu otsata Abisalomu. Ndipo ngakhale ngwazi imene mtima wake ukunga mtima wa mkango idzasungunuka konse, pakuti Aisraele onse adziwa atate wanu kuti ndiye munthu wamphamvu, ndi iwo ali naye ndiwo ngwazi. Koma uphungu wanga ndiwo kuti musonkhanitse Aisraele onse kwa inu kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba, monga mchenga uli panyanja kuchuluka kwao; ndi kuti mutuluke kunkhondo mwini wake. Chomwecho tidamvumbulukira pa malo akuti adzapezeka, ndipo tidzamgwera monga mame agwa panthaka, ndipo sitidzasiya ndi mmodzi yense wa iye ndi anthu onse ali naye. Ndiponso ngati walowa kumudzi wina, Aisraele onse adzabwera ndi zingwe kumudziko, ndipo tidzaukokera kumtsinje, kufikira sikapezeka kamwala kakang'ono kumeneko. Ndipo Abisalomu ndi anthu onse a Israele anati, Uphungu wa Husai Mwariki uposa uphungu wa Ahitofele. Pakuti kunaikidwa ndi Yehova kutsutsa uphungu wabwino wa Ahitofele kuti Yehova akamtengere Abisalomu choipa. Pomwepo Husai ananena ndi Zadoki ndi Abiyatara ansembewo, Ahitofele anapangira Abisalomu ndi akulu a Israele zakutizakuti; koma ine ndinapangira zakutizakuti. Chifukwa chake tsono mutumize msanga nimuuze Davide kuti Musagona usiku uno pa madooko a kuchipululu, koma muoloke ndithu, kuti mfumu ingamezedwe ndi anthu onse amene ali naye. Ndipo Yonatani ndi Ahimaazi anakhala ku Enirogele; mdzakazi ankapita kuwauza; ndipo iwo anapita nauza mfumu Davide, pakuti sangaoneke iwowo alikulowa m'mudzi. Koma mnyamata wina anawaona nauza Abisalomu; ndipo ajawo anachoka msanga onse awiri, nafika kunyumba ya munthu ku Bahurimu, amene anali nacho chitsime pabwalo pake; ndipo anatsikira m'menemo. Ndipo mkazi anatenga chivundikiro nachiika pakamwa pa chitsime, napapasapo lipande la tirigu; momwemo sichinadziwika. Ndipo anyamata a Abisalomu anafika kunyumba kwa mkaziyo; nati, Ali kuti Ahimaazi ndi Yonatani? Ndipo mkaziyo ananena nao, Anaoloka kamtsinje kamadzi. Ndipo atawafunafuna, osawapeza, anabwerera kunka ku Yerusalemu. Ndipo kunali, atapita iwo, ajawo anatuluka m'chitsime, namka nauza mfumu Davide; nati kwa Davide, Nyamukani nimuoloke madzi msanga; pakuti Ahitofele anapangira zotere pa inu. Pomwepo Davide ananyamuka ndi anthu onse amene anali naye, naoloka Yordani. Kutacha m'mawa sanasowe mmodzi wa iwo wosaoloka Yordani. Ndipo Ahitofele, pakuona kuti sautsata uphungu wake anamanga bulu wake, nanyamuka, nanka kumudzi kwao, nakonza za pa banja lake, nadzipachika, nafa, naikidwa m'manda a atate wake. Ndipo Davide anafika ku Mahanaimu. Abisalomu naoloka Yordani, iye ndi anthu onse a Israele pamodzi naye. Ndipo Abisalomu anaika Amasa, kazembe wa khamulo, m'malo a Yowabu. Koma Amasayu ndiye mwana wa munthu dzina lake Yetere Mwismaele, amene analowa kwa Abigaile, mwana wamkazi wa Nahasi, mlongo wa Zeruya, amai a Yowabu. Ndipo Israele ndi Abisalomu anamanga zithando m'dziko la Giliyadi. Ndipo kunali pakufika Davide ku Mahanaimu, Sobi mwana wa Nahasi wa ku Raba wa ana a Amoni, ndi Makiri mwana wa Amiyele wa ku Lodebara, ndi Barizilai Mgiliyadi wa ku Rogelimu, iwo anabwera nao makama, ndi mbale, ndi zotengera zadothi, ndi tirigu, ndi barele, ndi ufa, ndi tirigu wokazinga, ndi nyemba, ndi mphodza, ndi zokazinga zina, ndi uchi ndi mafuta, ndi nkhosa, ndi mase a ng'ombe, kuti adye Davide, ndi anthu amene anali naye; pakuti anati, Anthu ali ndi njala, olema, ndi aludzu m'chipululumo. Ndipo Davide anawerenga anthu amene anali naye, nawaikira atsogoleri a zikwi ndi atsogoleri a mazana. Davide natumiza anthu atawagawa magulu atatu, gulu limodzi aliyang'anire Yowabu, lina aliyang'anire Abisai, mwana wa Zeruya, mbale wa Yowabu, ndi lina aliyang'anire Itai Mgiti. Ndipo mfumu inanena ndi anthu, Zoonadi ine ndemwe ndidzatuluka limodzi ndi inu. Koma anthuwo anati, Simudzatuluka ndinu; pakuti tikathawa sadzatisamalira ife; ngakhale limodzi la magawo awiri a ife likafa sadzatisamalira; koma inu mulingana ndi zikwi khumi a ife; chifukwa chake tsono nkwabwino kuti mutithandize kutuluka m'mudzi. Ndipo mfumu inanena nao, Ndidzachita chimene chikomera inu. Mfumu niima pambali pa chipata, ndipo anthu onse anatuluka ali mazana, ndi zikwi. Ndipo mfumu inalamulira Yowabu ndi Abisai ndi Itai, kuti, Chifukwa cha ine muchite mofatsa ndi mnyamatayo, Abisalomu. Ndipo anthu onse anamva pamene mfumu inalamulira atsogoleriwo za Abisalomu. Chomwecho anthuwo anatulukira kuthengo kukamenyana ndi Israele; nalimbana ku nkhalango ya ku Efuremu. Ndipo anthu a Israele anakanthidwa pamenepo pamaso pa anyamata a Davide, ndipo kunali kuwapha kwakukulu kumeneko tsiku lomwelo, anthu zikwi makumi awiri. Pakuti nkhondo inatanda pa dziko lonse, ndipo tsiku lomwelo nkhalango inaononga anthu akuposa amene anaonongeka ndi lupanga. Ndipo Abisalomu anakomana ndi anyamata a Davide. Abisalomu naberekeka pa nyuru yake, ndipo nyuruyo inapita pansi pa nthambi zolimba za thundu wamkulu. Ndipo mutu wake unakodwa ndi mtengo, iye ali lende pakati pa thambo ndi pansi ndi nyuru imene inali pansi pa iye inapitirira. Ndipo munthu wina anamuona, nauza Yowabu, nati, Onani, ndaona Abisalomu ali lende pathundu. Ndipo Yowabu ananena ndi womuuzayo, Ndipo taona, unamuona, tsono unalekeranji kumkantha agwe pansi pomwepo? Ndipo ine ndikadakupatsa ndalama khumi ndi lamba. Munthuyo nanena ndi Yowabu, Ndingakhale ndikalandira ndalama chikwi m'dzanja langa, koma sindikadasamula dzanja langa pa mwana wa mfumu; pakuti m'kumva kwathu mfumu inalamulira inu ndi Abisai ndi Itai, kuti, Chenjerani munthu yense asakhudze mnyamatayo Abisalomu. Ndikadachita chonyenga pa moyo wake, palibe mlandu ubisika kwa mfumu; ndipo inu nomwe mukadanditsutsa. Pomwepo Yowabu anati, Sindiyenera kuchedwa nawe. Natenga mikondo itatu nagwaza nayo mtima wa Abisalomu alikukhala wamoyo pakati pa mtengowo. Ndipo anyamata khumi onyamula zida zake za Yowabu anamzungulira Abisalomu namkantha namupha. Ndipo Yowabu analiza lipenga, ndipo anthu anabwerera naleka kupirikitsa Aisraele; pakuti Yowabu analetsa anthuwo. Ndipo anatenga Abisalomu namponya m'chidzenje chachikulu kunkhalangoko; naunjika pamwamba pake mulu waukulu ndithu wamiyala; ndipo Aisraele onse anathawa yense ku hema wake. Koma Abisalomu akali moyo adatenga nadziutsira choimiritsacho chili m'chigwa cha mfumu; pakuti anati, Ndilibe mwana wamwamuna adzakhala chikumbutso cha dzina langa; natcha choimiritsacho ndi dzina la iye yekha; ndipo chitchedwa chikumbutso cha Abisalomu, kufikira lero lomwe. Pomwepo Ahimaazi mwana wa Zadoki anati, Ndithamange nditengere mfumu mau kuti Yehova wabwezera chilango adani ake. Ndipo Yowabu ananena naye, Sudzakhala iwe wotengera mau lero, koma tsiku lina udzatengera mau; koma lero sudzatengera mau, chifukwa mwana wa mfumu wafa. Pamenepo Yowabu ananena ndi Mkusi, Kauze mfumu zimene unaziona. Ndipo Mkusi anawerama kwa Yowabu, nathamanga. Ndipo Ahimaazi mwana wa Zadoki ananena kachiwiri kwa Yowabu, Komatu, mundilole ndithamange inenso kutsata Mkusi. Ndipo Yowabu anati, Udzathamangiranji, mwana wanga, popeza sudzalandira mphotho ya pa mauwo? Koma ngakhale kotero, anati iye, Ndithamange. Iye nanena naye, Thamanga. Ndipo Ahimaazi anathamanga njira ya kuchigwa, napitirira Mkusi. Koma Davide anakhala pakati pa zipata ziwiri; ndipo mlonda anakwera pa tsindwi la chipata cha kulinga, natukula maso ake, napenya; naona munthu alikuthamanga yekha. Pamenepo mlondayo anafuula, nauza mfumu. Mfumuyo niti, Ngati ali yekha alikubwera ndi mau. Ndipo iye uja anayenda msanga, nayandikira. Ndipo mlondayo anaona munthu wina wothamanga; mlonda naitana wakuchipata nanena, Taona munthu wina wakuthamanga yekha. Ndipo mfumu inati, Iyenso abwera ndi mau. Mlondayo nati, Ndiyesa kuti kuthamanga kwa wapatsogoloyo kunga kuthamanga kwa Ahimaazi mwana wa Zadoki. Ndipo mfumu inati, Iye ndiye munthu wabwino, alikubwera ndi mau okoma. Ndipo Ahimaazi anafuula, nanena ndi mfumu, Mtendere. Ndipo anawerama pamaso pa mfumu ndi nkhope yake pansi, nati, Alemekezeke Yehova Mulungu wanu amene anapereka anthu akukwezera dzanja lao pa mbuye wanga mfumu. Ndipo mfumu inati, Kodi mnyamatayo Abisalomu ali bwino? Ahimaazi nayankha, Pamene Yowabu anatumiza mnyamata wa mfumu, ndiye ine mnyamata wanu, ndinaona piringupiringu, koma sindinadziwa ngati kutani. Ndipo mfumu inati, Patuka nuime apa. Napatuka, naimapo. Ndipo onani, Mkusiyo anafika, nati, Mau akuuza mbuye wanga mfumu; pakuti Yehova anabwezera chilango lero onse akuukira inu. Ndipo mfumu inanena ndi Mkusiyo, Mnyamatayo Abisalomu ali bwino? Mkusiyo nayankha, Adani a mbuye wanga mfumu, ndi onse akuukira inu kukuchitirani zoipa, akhale monga mnyamata ujayo. Ndipo mfumuyo inagwidwa chisoni, nikwera ku chipinda chosanja pa chipatacho, nilira misozi; niyenda, nitero, Mwana wanga Abisalomu, mwana wanga Abisalomu; mwana wanga! Mwenzi nditakufera ine, Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga! Ndipo anauza Yowabu, Onani mfumu ilikulira misozi, nilira Abisalomu. Ndipo chipulumutso cha tsiku lija chinasandulika maliro kwa anthu onse; pakuti anthu anamva kuti, Mfumu ili ndi chisoni chifukwa cha mwana wake. Ndipo tsiku lija anthu analowa m'mudzi kachetechete, monga azemba anthu akuchita manyazi pakuthawa nkhondo. Ndipo mfumu inafunda nkhope yake, nilira ndi mau okweza, Mwana wanga Abisalomu, Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga, Ndipo Yowabu anafika kunyumba ya mfumu, nati, Lero mwachititsa manyazi nkhope zao za anyamata anu onse, amene anapulumutsa moyo wanu lero, ndi miyoyo ya ana anu aamuna ndi aakazi, ndi miyoyo ya akazi anu, ndi miyoyo ya akazi anu ang'ono; m'mene mukonda awo akudana nanu, ndi kudana nao amene akukondani. Pakuti lero mwalalikira kuti simusamalira konse akalonga ndi anyamata; pakuti lero ndizindikira kuti tikadafa ife tonse, ndipo akadakhala ndi moyo Abisalomu, pamenepo mukadakondwera ndithu. Chifukwa chake tsono nyamukani, mutuluke, nimulankhule zowakondweretsa anyamata anu; pakuti ndilumbira, Pali Yehova, kuti mukapanda kutuluka inu, palibe munthu mmodzi adzakhala nanu usiku uno; ndipo chimenechi chidzakuipirani koposa zoipa zonse zinakugwerani kuyambira ubwana wanu kufikira tsopanoli. Pamenepo mfumu inanyamuka, nikakhala pachipata. Ndipo inauza anthu kuti, Onani mfumu ilikukhala pachipata; anthu onse nadza pamaso pa mfumu. Koma Aisraele adathawa, munthu yense ku hema wake. Ndipo anthu onse a m'mafuko onse a Israele analikutsutsana, ndi kuti, Mfumuyo inatilanditsa ife m'dzanja la adani athu, natipulumutsa m'dzanja la Afilisti; ndipo tsopano inathawa m'dziko kuthawa Abisalomu. Ndipo Abisalomu amene tinamdzoza mfumu yathu anafa kunkhondo. Chifukwa chake tsono mulekeranji kunena mau akuti abwere nayo mfumuyo? Ndipo mfumu Davide anatumiza kwa Zadoki ndi Abiyatara ansembewo, nati, Mulankhule nao akulu a Yuda, kuti, Mukhale bwanji am'mbuyo kubwera nayo mfumu kunyumba yake? Pakuti mau a Aisraele onse anafika kwa mfumu akuti abwere nayo kunyumba yake. Inu ndinu abale anga, muli fupa langa ndi mnofu wanga; chifukwa ninji tsono muli am'mbuyo koposa onse kubwera nayo mfumu? Ndipo munene ndi Amasa, Suli fupa langa ndi mnofu wanga kodi? Mulungu andilange naonjezepo ngati sudzakhala chikhalire kazembe wa khamu la ankhondo pamaso panga, m'malo mwa Yowabu. Ndipo iye anakopa mitima ya anthu onse a Yuda, monga munthu mmodzi, natumiza iwo kwa mfumu, nati, Mubwere inu ndi anyamata anu onse. Chomwecho mfumu inabwera nifika ku Yordani. Ndipo Ayuda anadza ku Giligala, kuti akakomane ndi mfumu, ndi kumuolotsa mfumu pa Yordani. Ndipo Simei, mwana wa Gera, Mbenjamini, wa ku Bahurimu, anafulumira natsika pamodzi ndi anthu a Yuda kuti akakomane ndi mfumu Davide. Ndipo anali nao anthu chikwi chimodzi Abenjamini, ndi Ziba mnyamata wa nyumba ya Saulo; ndi ana ake amuna khumi ndi asanu, ndi anyamata ake makumi awiri pamodzi naye; iwo naoloka Yordani pamaso pa mfumu. Ndipo ngalawa yakuolotsera inaoloka kuti akatenge banja la mfumu ndi kuchita chomkomera. Ndipo Simei mwana wa Gera anagwa pansi pamaso pa mfumu pakuoloka iye pa Yordani. Nati kwa mfumu, Mbuye wanga asandiwerengere ine mphulupulu ndiponso musakumbukire chimene mnyamata wanu ndinachita mwamphulupulu tsiku lija mbuye wanga mfumu anatuluka ku Yerusalemu, ngakhale kuchisunga mumtima mfumu. Pakuti mnyamata wanu ndidziwa kuti ndinachimwa; chifukwa chake, onani, ndinadza lero, ndine woyamba wa nyumba yonse ya Yosefe kutsika kuti ndikomane ndi mbuye wanga mfumu. Koma Abisai mwana wa Zeruya anayankha nati, Kodi sadzaphedwapo Simei chifukwa cha kutemberera wodzozedwa wa Yehova? Koma Davide anati, Ndili ndi chiyani inu, ana a Zeruya inu, kuti muzikhala akutsutsana ndi ine lero? Kodi munthu adzaphedwa m'Israele lero? Sindidziwa kodi kuti ndine mfumu ya Israele lero? Ndipo mfumu inanena ndi Simei, Sudzafa. Mfumu nimlumbirira iye. Ndipo Mefiboseti mwana wa Saulo anatsika kukakomana ndi mfumu; ndipo sadasamba mapazi ake, kapena kumeta ndevu zake, kapena kutsuka zovala zake kuyambira tsiku lomuka mfumu kufikira tsiku lobwera kwao mumtendere. Ndipo kunali pakufika iye ku Yerusalemu kukakomana ndi mfumu, mfumu inanena naye, Chifukwa ninji sunapita nane Mefiboseti? Ndipo anayankha, Mbuye wanga mfumu, mnyamata wanga anandinyenga; pakuti mnyamata wanu ndinati, Ndidzadzimangira bulu kuti ndiberekekepo ndi kupita ndi mfumu, pakuti mnyamata wanu ndili wopunduka. Ndipo iye anandinamizira mnyamata wanu kwa mbuye wanga mfumu; koma mbuye wanga mfumu ali ngati mthenga wa Yehova; chifukwa chake chitani chimene chikukomerani. Pakuti nyumba yonse ya atate wanga inali anthu oyenera imfa pamaso pa mbuye wanga mfumu; koma inu munaika mnyamata wanu pakati pa iwo akudya pa gome lanu. Kuyenera kwanga nkutaninso kuti ndikaonjezere kudandaulira kwa mfumu? Ndipo mfumu inanena naye, Ulikulankhulanso bwanji za zinthu zako? Ine ndikuti, Iwe ndi Ziba mugawe dzikolo. Ndipo Mefiboseti anati kwa mfumu, Lingakhale lonselo alitenge, popeza mbuye wanga mfumu wabwera mumtendere kunyumba yake. Ndipo Barizilai, Mgiliyadi anatsika kuchokera ku Rogelimu; nayambuka pa Yordani ndi mfumu, kuti akamuolotse pa Yordani. Ndipo Barizilai anali nkhalamba, ndiye wa zaka makumi asanu ndi atatu; ndiye amene anapereka chakudya kwa mfumu muja anagona ku Mahanaimu, pakuti anali munthu womveka ndithu. Ndipo mfumu inanena ndi Barizilai, Tiyeni muoloke nane, ndipo ndidzakusungani pamodzi ndi ine ku Yerusalemu. Koma Barizilai ananena ndi mfumu, Masiku a zaka za moyo wanga ndiwo angati, kuti ndiyenera kukwera ndi mfumu kunka ku Yerusalemu? Lero ndili nazo zaka makumi asanu ndi atatu; kodi ndikhoza kuzindikiranso kusiyanitsa zabwino ndi zoipa? Mnyamata wanu ndikhoza kodi kuzindikira chimene ndidya kapena kumwa? Kodi ndikhozanso kumva mau a amuna ndi akazi oimba? Chifukwa ninji tsono mnyamata wanu ndidzakhalanso wolemetsa mbuye wanga mfumu. Mnyamata wanu angofuna kuoloka Yordani pamodzi ndi mfumu; ndipo afuniranji mfumu kundibwezerapo mphotho yotere? Mulole mnyamata wanu ndibwererenso, kuti ndikamwalire m'mudzi wanga kumanda a atate wanga ndi mai wanga. Koma suyu, Kimuhamu mnyamata wanu, iye aoloke pamodzi ndi mbuye wanga mfumu, ndipo mumchitire chimene chikukomerani. Ndipo mfumu inayankha, Kimuhamu adzaoloka nane, ndipo ndidzamchitira chimene chikukomereni; ndipo chilichonse mukadzapempha kwa ine ndidzakuchitirani inu. Ndipo anthu onse anaoloka Yordani, ndi mfumu yomwe inaoloka; ndipo mfumuyo inapsompsona Barizilai nimdalitsa; ndipo iye anabwerera kunka kumalo kwake. Chomwecho mfumu inaoloka nifika ku Giligala, ndi Kimuhamu anaoloka naye, ndipo anthu onse a Yuda adaolotsa mfumu, ndiponso gawo lina la anthu a Israele. Ndipo onani, Aisraele onse anafika kwa mfumu, nanena ndi mfumu, Abale athu anthu a Yuda anakuchotsani bwanji mwakuba, naolotsa mfumu ndi banja lake pa Yordani, ndi anthu onse a Davide pamodzi naye? Ndipo anthu onse a Yuda anayankha anthu a Israele. Chifukwa mfumu ili ya chibale chathu; tsono mulikukwiyiranji pa mlandu umenewu? Tinadya konse za mfumu kodi? Kapena kodi anatipatsa mtulo uliwonse? Ndipo anthu a Israele anayankha anthu a Yuda, nati, Ife tili ndi magawo khumi mwa mfumu, ndi mwa Davide koposa inu; chifukwa ninji tsono munatipeputsa ife, osayamba kupangana nafe za kubwezanso mfumu yathu? Koma mau a anthu a Yuda anali aukali koposa mau a anthu a Israele. Ndipo kudangotero kuti pamenepo panali munthu woipa, dzina lake ndiye Sheba mwana wa Bikiri Mbenjamini; naliza iye lipenga, nati, Ife tilibe gawo mwa Davide, tilibenso cholowa mwa mwana wa Yese; munthu yense apite ku mahema ake, Israele inu. Chomwecho anthu onse a Israele analeka kutsata Davide, natsata Sheba mwana wa Bikiri; koma anthu a Yuda anaphatikizana ndi mfumu yao, kuyambira ku Yordani kufikira ku Yerusalemu. Ndipo Davide anafika kunyumba kwake ku Yerusalemu. Mfumuyo nitenga akazi khumi ang'onowo amene adawasiya asunge nyumbayo, nawatsekera m'nyumba, nawapatsa chakudya, koma sanalowane nao. Chomwecho iwowa anatsekedwa kufikira tsiku la imfa yao, nakhala ngati akazi amasiye. Pamenepo mfumu inati kwa Amasa, Undiitanire anthu a Yuda asonkhane asanapite masiku atatu, nukhale pano iwenso. Chomwecho Amasa anamuka kukaitana anthu a Yuda asonkhane; koma anachedwa, napitiriza nthawi imene idamuikira. Ndipo Davide anati kwa Abisai, Tsopano Sheba mwana wa Bikiri adzatichitira choipa choposa chija cha Abisalomu; utenge anyamata a mbuye wako numtsatire, kuti angapeze midzi ya malinga ndi kupulumuka osaonekanso. Ndipo anatuluka namtsata anthu a Yowabu, ndi Akereti ndi Apeleti, ndi anthu onse amphamvu; natuluka m'Yerusalemu kukalondola Sheba mwana wa Bikiri. Pamene anafika iwo pa mwala waukulu uli ku Gibiyoni, Amasa anadza kukomana nao. Ndipo Yowabu atavala mwinjiro wake, anadzimangirira lamba lolongamo lupanga m'chimake m'chuuno mwake; ndipo m'kuyenda kwake lidasololoka. Ndipo Yowabu ananena ndi Amasa, Uli bwino mbale wanga? Ndipo Yowabu anagwira ndevu za Amasa ndi dzanja lake lamanja kuti ampsompsone. Koma Amasa sanasamalire lupanga lili m'dzanja la Yowabu; chomwecho iye anamgwaza nalo m'mimba; nakhuthula matumbo ake pansi, osamgwazanso, nafa iye. Ndipo Yowabu ndi Abisai mbale wake analondola Sheba mwana wa Bikiri. Ndipo mnyamata wina wa Yowabu anaima pali iye, nati, Wovomereza Yowabu, ndi iye amene ali wake wa Davide, atsate Yowabu. Ndipo Amasa analikukunkhulira m'mwazi wake pakati pa mseu. Ndipo pamene munthuyo anaona kuti anthu onse anaima, iye ananyamula Amasa namchotsa pamseu kunka naye kuthengo, namfunda ndi chovala, pamene anaona kuti anaima munthu yense wakufika pali iye. Atamchotsa iye mumseu, anthu onse anapitirira kumtsata Yowabu kukalondola Sheba mwana wa Bikiri. Ndipo anapyola mafuko onse a Israele kufikira ku Abele ndi ku Betimaaka, ndi kwa Abikiri onse; iwo nasonkhana pamodzi namlondolanso. Ndipo anadza nammangira misasa m'Abele wa Betimaaka, naundira nthumbira pa mudziwo, ndipo unagunda linga; ndipo anthu onse akukhala ndi Yowabu anakumba lingalo kuti aligwetse. Pamenepo mkazi wanzeru wa m'mudzimo anafuula, kuti, Imvani, imvani; munene kwa Yowabu, Bwerani pafupi kuno kuti ndilankhule nanu. Ndipo anayandikira kwa mkaziyo; ndi mkaziyo anati, Ndinu Yowabu kodi? Iye nayankha, Ndine amene. Pamenepo ananena naye, Imvani mau a mdzakazi wanu. Iye nayankha, Ndilikumva. Ndipo iye analankhula, nati, Kale adanena kuti, Zoonadi adzapempha uphungu ku Abele; ndipo potero mlandu udatha. Ine ndine wa awo amene ali amtendere ndi okhulupirika m'Israele; inu mulikufuna kuononga mudzi ndi mai wa m'Israele; mudzamezeranji cholowa cha Yehova? Ndipo Yowabu anayankha nati, Iai ndi pang'ono ponse, chikhale kutali kwa ine, kuti ndingameze ndi kuononga. Mlanduwo suli wotere ai, koma munthu wa ku dziko lamapiri la Efuremu, dzina lake ndiye Sheba mwana wa Bikiri, anakweza dzanja lake pa mfumu Davide; mpereke iye yekha ndipo ndidzachoka kumudzi kuno. Ndipo mkaziyo anati kwa Yowabu, Onani tidzakuponyerani mutu wake kutumphitsa linga. Pomwepo mkaziyo anapita kwa anthu onse mwa nzeru yake. Ndipo iwo anadula mutu wa Sheba mwana wa Bikiri, nauponya kunja kwa Yowabu. Ndipo analiza lipenga, nabalalika kuchoka pamudzipo, munthu yense kunka ku hema wake. Ndipo Yowabu anabwerera kunka ku Yerusalemu kwa mfumu. Ndipo Yowabu anali woyang'anira khamu lonse la Israele; ndi Benaya, mwana wa Yehoyada, anayang'anira Akereti ndi Apeleti; ndi Adoramu anayang'anira msonkho; ndi Yehosafati mwana wa Ahiludi anali wolemba mbiri; ndi Seva anali mlembi; ndi Zadoki ndi Abiyatara anali ansembe; ndiponso Ira Myairi anali ansembe a Davide. Ndipo m'masiku a Davide munali njala, zaka zitatu; ndipo Davide anafunsira kwa Yehova. Ndipo Yehova anati, Ndicho chifukwa cha Saulo ndi nyumba yake yamwazi, popeza iye anawapha Agibiyoni. Ndipo mfumu inaitana Agibiyoni, ninena nao (koma Agibiyoni, sanali a ana a Israele, koma a Aamori otsala; ndipo ana a Israele anawalumbirira kwa iwo, koma Saulo anafuna kuwapha mwa changu chake cha kwa ana a Israele ndi a Yuda). Ndipo Davide ananena ndi Agibiyoni, Ndidzakuchitirani chiyani, ndipo ndidzakuyanjanitsani ndi chiyani kuti mukadalitse cholowa cha Yehova? Ndipo Agibiyoni ananena naye, Sitifuna siliva kapena golide wa Saulo kapena nyumba yake; ndiponso sitifuna kupha munthu aliyense wa m'Israele. Nati iye, Monga inu mudzanena, momwemo ndidzakuchitirani. Ndipo anati kwa mfumu, Munthu uja anatitha natilingalira pa ife chotionongera kuti tisakhalenso m'malire ali onse a Israele. Mutipatse ana ake amuna asanu ndi awiri, ndipo tidzawapachika kwa Yehova m'Gibea wa Saulo, wosankhika wa Yehova. Mfumu niti, Ndidzawapereka. Koma mfumu inaleka Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, chifukwa cha lumbiro la kwa Yehova linali pakati pa Davide ndi Yonatani mwana wa Saulo. Koma mfumu inatenga ana amuna awiri a Rizipa mwana wamkazi wa Aya, amene anambalira Saulo, ndiwo Arimoni ndi Mefiboseti; ndiponso ana amuna asanu a Mikala, mwana wamkazi wa Saulo, amene iye anambalira Adriyele mwana wa Barizilai Mmehola; niwapereka m'manja a Agibiyoni, iwo nawapachika m'phiri pamaso pa Yehova, ndipo anagwa pamodzi onse asanu ndi awiri; m'masiku a kukolola, m'masiku oyamba, poyamba kucheka barele. Ndipo Rizipa mwana wamkazi wa Aya anatenga chiguduli, nadziyalira ichi pathanthwe, kuyambira pakukolola kufikira madzi ochokera kumwamba adawagwera; ndipo sadalola mbalame za m'mlengalenga kutera pa iwo usana, kapena zilombo za kuthengo usiku. Ndipo anauza Davide chimene Rizipa mwana wamkazi wa Aya, mkazi wamng'ono wa Saulo anachita. Ndipo Davide ananka natenga mafupa a Saulo ndi mafupa a Yonatani mwana wake kwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi amene anawaba m'khwalala la Beteseani, kumene Afilisti adawapachika, tsiku lija Afilistiwo anapha Saulo ku Gilibowa; nachotsa kumeneko mafupa a Saulo ndi mafupa a Yonatani mwana wake; nasonkhanitsa iwo mafupa a iwo aja adapachikidwa. Naika mafupa a Saulo ndi Yonatani mwana wake ku dziko la Benjamini m'Zela, m'manda a Kisi atate wake; nachita zonse inalamulira mfumu. Ndipo pambuyo pake Mulungu anapembedzeka za dzikolo. Ndipo Afilisti anaponyananso nkhondo ndi Aisraele; ndipo Davide anatsika ndi anyamata ake pamodzi naye naponyana ndi Afilisti; nafuna kukomoka Davide. Ndipo Isibi-Benobi, ndiye wa ana a Rafa, amene kulemera kwa mkondo wake kunali masekeli mazana atatu a mkuwa, iyeyo anavala lupanga latsopano, nati aphe Davide. Koma Abisai mwana wa Zeruya anamthandiza namkantha Mfilistiyo, namupha. Pomwepo anthu a Davide anamlumbirira iye nati, Inu simudzatuluka nafenso kunkhondo, kuti mungazime nyali ya Israele. Ndipo kunali chitapita ichi, kunalinso nkhondo ndi Afilisti ku Gobu; pamenepo Sibekai Muhusa anapha Safi, ndiye wa ana a Rafa. Ndipo panalinso nkhondo ndi Afilisti ku Gobu; ndipo Elihanani mwana wa Yaare-Oregimu wa ku Betelehemu anapha Goliyati Mgiti, amene mtengo wa mkondo wake unanga mtanda wa woombera nsalu. Ndipo panalinso nkhondo ku Gati, kumene kunali munthu wa msinkhu waukulu, amene anali nazo zala zisanu ndi chimodzi pa dzanja lonse, ndi pa phazi lonse zala zisanu ndi chimodzi, kuwerenga kwa zonse ndiko makumi awiri ndi zinai; ndipo iyenso anambala ndi Rafa. Ndipo pakutonza Israele iyeyu, Yonatani mwana a Simea mbale wa Davide anamupha. Awa anai anawabala ndi Rafa ku Gati; ndipo anagwa ndi dzanja la Davide ndi la anyamata ake. Ndipo Davide analankhula kwa Yehova mau a nyimbo iyi tsikuli Yehova anampulumutsa m'dzanja la adani ake onse, ndi m'dzanja la Saulo. Ndipo anati, Yehova ndiye thanthwe langa, ndi ngaka yanga, ndi Mpulumutsi wanga, wangadi. Mulungu wa thanthwe langa, Iye ndidzamkhulupirira; chikopa changa, ndi nyanga ya chipulumutso changa, nsanja yanga yaitali, ndi populumukirapo panga; Mpulumutsi wanga, mundipulumutsa kuchiwawa. Ndidzaitana kwa Yehova amene ayenera timtamande; chomwecho ndidzapulumutsidwa kwa adani anga. Pakuti mafunde a imfa anandizinga, mitsinje ya zopanda pake inandiopsa ine. Zingwe za kumanda zinandizingira; misampha ya imfa inandifikira ine. M'kusauka kwanga ndinaitana kwa Yehova, inde ndinakuwira kwa Mulungu wanga; ndipo Iye anamva mau anga ali m'Kachisi wake, ndi kulira kwanga kunafika ku makutu ake. Pomwepo dziko linagwedezeka ndi kunthunthumira. Maziko a dziko la kumwamba anasunthika. Nagwedezeka, chifukwa Iye anakwiya. M'mphuno mwake munatuluka utsi, ndi moto wotuluka m'kamwa mwake unaononga; makala anayaka nao. Anaweramitsa miyambanso, natsika; ndipo mdima wandiweyani unali pansi pa mapazi ake. Ndipo Iye anaberekeka pa kerubi nauluka; inde anaoneka pa mapiko a mphepo. Ndipo anayesa mdimawo ngati mahema omzungulira Iye, kusonkhana kwa madzi ndi mitambo yochindikira ya mlengalenga. Cheza cha pamaso pake makala a moto anayaka. Yehova anagunda kumwamba; ndipo Wam'mwambamwamba ananena mau ake. Ndipo Iye anatumiza mivi, nawawaza; mphezi, nawaopsa. Pamenepo m'munsi mwa nyanja munaoneka, maziko a dziko anaonekera poyera, ndi mtonzo wa Yehova, ndi mpumo wa mpweya wa m'mphuno mwake. Iye anatumiza kuchokera kumwamba nanditenga; Iye ananditulutsa m'madzi aakulu. Iye anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu, kwa iwo akudana ndi ine; pakuti anandiposa mphamvu. Anandifikira ine tsiku la tsoka langa; koma Yehova anali mchirikizo wanga. Iye ananditulutsanso ku malo akulu; Iye anandipulumutsa, chifukwa akondwera ndi ine. Yehova anandibwezera monga mwa cholungama changa; monga mwa kuyera kwa manja anga anandipatsa mphotho. Pakuti ndinasunga njira za Yehova, osapatukira ku zoipa kusiya Mulungu wanga. Pakuti maweruzo ake onse anali pamaso panga; ndipo za malemba ake, sindinawapatukira. Ndinakhalanso wangwiro kwa Iye, ndipo ndinadzisunga kusachita kuipa kwanga. Chifukwa chake Yehova anandibwezera monga mwa cholungama changa; monga mwa kuyera kwanga pamaso pake. Ndi chifundo Inu mudzadzionetsa wachifundo, ndi munthu wangwiro mudzadzionetsa wangwiro. Ndi oyera mtima mudzadzionetsa woyera mtima; ndi otsutsatsutsa mudzadzionetsa wopotoza. Ndipo mudzapulumutsa anthu osautsidwa; koma maso anu ali pa odzikuza kuti muwachepetse. Pakuti Inu ndinu nyali yanga, Yehova; ndipo Yehova adzaunika mumdima mwanga. Pakuti ndi Inu ndithamangira gulu; ndi Mulungu wanga ndilumphira linga. Kunena za Mulungu, njira yake ili yangwiro; mau a Yehova anayesedwa; Iye ndiye chikopa kwa onse akukhulupirira Iye. Pakuti Mulungu ndani, koma Yehova? Ndipo thanthwe ndani, koma Mulungu wathu? Mulungu ndiye linga langa lamphamvu; ndipo Iye ayendetsa angwiro mu njira yake. Iye asandutsa mapazi ake akunga mapazi a mbawala; nandiika pa misanje yanga. Iye aphunzitsa manja anga nkhondo; kotero kuti manja anga alifula uta wamkuwa. Ndiponso munandipatsa chikopa cha chipulumutso chanu; ndi kufatsa kwanu kunandikulitsa. Munakulitsa kulunza kwanga pansi panga, ndi mapazi anga sanaterereke. Ndinapirikitsa adani anga, ndi kuwaononga; ndiponso sindinabwerera mpaka nditawatha. Ndinawatha ndi kuwapyoza, kuti sakhoza kuuka, inde anagwa pansi pa mapazi anga. Pakuti Inu munandimanga m'chuuno ndi mphamvu ya kunkhondo; munandigonjetsera akundiukira. Munatembenuzitsanso adani anga andipatse mbuyo, kuti ndiwalikhe akudana ndi ine. Anayang'ana iwo, koma panalibe wopulumutsa; ngakhale kwa Yehova, koma Iye sanawayankhe. Pomwepo ndinawasansantha asalale ngati fumbi la padziko, ndinawapondereza ngati dothi la m'makwalala. Inunso munandipulumutsa ine pa kulimbana kwa anthu anga; munandisunga ndikhale mutu wa amitundu; Anthu amene sindinawadziwa adzanditumikira ine. Alendo adzandigonjera ine, pakumva za ine, adzandimvera pomwepo. Alendo adzafota, nadzabwera ndi kunthunthumira otuluka mokwiririka mwao. Yehova ali ndi moyo; ndipo lidalitsike thanthwe langa; ndipo akulitsidwe Mulungu wa thanthwe la chipulumutso changa; inde Mulungu wakundibwezera chilango ine, ndi kundigonjetsera anthu a mitundu. Amene anditulutsa kwa adani anga; inde mundikweza ine pamwamba pa iwo akundiukira; mundipulumutsa kwa munthu wachiwawa. Chifukwa chake ndidzakuongani Yehova, pakati pa amitundu, ndipo ndidzaimba zolemekeza dzina lanu. Iye apatsa mfumu yake chipulumutso chachikulu; naonetsera chifundo wodzozedwa wake, kwa Davide ndi mbeu yake ku nthawi zonse. Ndipo mau otsiriza a Davide ndi awa, Atero Davide mwana wa Yese, atero munthu wokwezedwa, ndiye wodzozedwa wa Mulungu wa Yakobo, ndi mwini nyimbo yokoma ya Israele. Mzimu wa Yehova unalankhula mwa ine, ndi mau ake anali pa lilime langa. Mulungu wa Israele anati, Thanthwe la Israele linalankhula ndi ine; kudzakhala woweruza anthu molungama; woweruza m'kuopa Mulungu. Iye adzakhala ngati kuunika kwa m'mawa, potuluka dzuwa, M'mawa mopanda mitambo; pamene msipu uphuka kutuluka pansi, chifukwa cha kuwala koyera, italeka mvula. Zoonadi nyumba yanga siikhala yotere ndi Mulungu; koma Iye anapangana ndi ine pangano losatha, lolongosoka mwa zonse ndi losungika; pakuti ichi ndi chipulumutso changa chonse, ndi kufuma kwanga konse, kodi sadzachimeretsa? Koma oipa onse adzakhala ngati minga yoyenera kuitaya, pakuti siigwiridwa ndi dzanja; koma wakukhudza iyo adzikonzeratu chitsulo ndi luti la mkondo; ndipo idzatenthedwa konse ndi moto m'malo mwao. Maina a ngwazi Davide anali nazo ndiwo: Yosebu-Basebeti Mtakemoni, mkulu wa akazembe; ameneyu ndiye Adino Mwezni wolimbana ndi mazana atatu ophedwa nthawi imodzi. Ndipo wotsatana naye Eleazara mwana wa Dodo mwana wa Mwahohi, mmodzi wa ngwazi zitatu zokhala ndi Davide pamene iwo anatonza Afilisti osonkhanidwa kunkhondo kumeneko, atachoka Aisraele; iye ananyamuka, nakantha Afilisti kufikira dzanja lake linalema, ndi dzanja lake lomamatika kulupanga; ndipo Yehova anachititsa chipulumutso chachikulu tsiku lija, ndipo anthu anabwera m'mbuyo mwake kukafunkha kokha. Ndipo wotsatana naye ndiye Sama mwana wa Age Muharari. Ndipo Afilisti anasonkhana ali gulu pa Lehi pamene panali munda wamphodza; anthu nathawa Afilistiwo. Koma iyeyo anaima pakati pa mundawo, nautchinjiriza, napha Afilistiwo. Ndipo Yehova anachititsa chipulumutso chachikulu. Ndipo atatu a mwa makamu atatu opambanawo, anatsika nafika kwa Davide nyengo ya kukolola m'phanga la ku Adulamu; ndi gulu la Afilisti linamanga zithando m'chigwa cha Refaimu. Pamenepo Davide anali m'linga, ndi boma la Afilisti linali m'Betelehemu. Ndipo Davide analakalaka nati, Ha! Wina akadandipatsa madzi a m'chitsime cha ku Betelehemu chili pachipatapo! Ndipo ngwazi zitatuzo zinapyola khamu la Afilisti, nizitunga madzi m'chitsime cha ku Betelehemu, cha pa chipatacho, nawatenga, nafika nao kwa Davide; koma iye sanafune kumwako, koma anawathira pansi kwa Yehova. Nati, Ndisachite ichi ndi pang'ono ponse, Yehova; ndimwe kodi mwazi wa anthu awa anapitawa ndi kutaya moyo wao? Chifukwa chake iye anakana kumwa. Izi anazichita ngwazi zitatuzi. Ndipo Abisai, mbale wa Yowabu, mwana wa Zeruya, anali wamkulu wa atatuwa. Iye natukula mkondo wake pa anthu mazana atatu nawapha, natenga dzina iye mwa atatuwa. Kodi iye sindiye waulemu mwa atatuwa? Chifukwa chake anali kazembe wao; ngakhale iyenso sadafikana ndi atatu oyamba. Ndipo Benaya, mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi wa ku Kabizeeli amene anachita zamphamvu; iye anapha anthu awiri a Mowabu akunga mikango, natsikanso iye napha mkango m'mbuna nyengo ya chipale chofewa; ndipo anapha Mwejipito munthu wokongola, Mwejipito anali nao mkondo m'dzanja lake; koma iyeyo anatsikira kwa iye ndi ndodo, nasolola mkondowo m'dzanja la Mwejipito, namupha ndi mkondo wa iye mwini. Izi anachita Benaya mwana wa Yehoyada, natenga dzina mwa ngwazi zitatuzo. Iye ndiye waulemu koposa makumi atatuwo, koma sadafikana ndi atatu oyamba. Ndipo Davide anamuika kuyang'anira olindirira ake. Asahele mbale wa Yowabu anali wa makumi atatuwo; Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu; Sama Mharodi, Elika Mharodi; Helezi Mpaliti, Ira mwana wa Ikesi Mtekowa. Abiyezere Mwanatoti, Mebunai Muhusa; Zalimoni Mwahohi, Maharai Mnetofa; Helebi mwana wa Baana Mnetofa, Itai mwana wa Ribai wa ku Gibea wa ana a Benjamini; Benaya Mpiratoni, Hidai wa ku timitsinje ta Gaasi; Abiyaliboni Mwarabati, Azimaveti Mbahurimi; Eliyaba Msaaliboni wa ana a Yaseni, Yonatani; Sama Muharari, Ahiyamu mwana wa Sarara Muharari; Elifeleti mwana wa Ahasibai, mwana wa Mmaaka, Eliyamu mwana wa Ahitofele Mgiloni; Heziro wa ku Karimele, Paarai Mwaraba; Igala mwana wa Natani wa ku Zoba, Bani Mgadi; Zeleki Mwamoni, Naharai Mbeeroti, onyamula zida za Yowabu mwana wa Zeruya; Ira Mwitiri, Garebu Mwitiri; Uriya Muhiti; onse pamodzi anali makumi atatu mphambu asanu ndi awiri. Ndipo mkwiyo wa Yehova unayakanso pa Israele, nafulumiza Davide pa iwo, nati, Muka, nuwerenge Israele ndi Yuda. Ndipo mfumu inanena ndi Yowabu kazembe wa khamu, amene anali naye, Kayendere tsopano mafuko onse a Israele, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba, nuwerenge anthuwo, kuti ndidziwe kuchuluka kwao kwa anthu. Ndipo Yowabu ananena ndi mfumu, Yehova Mulungu wanu aonjezere kwa anthu monga ali kuwachulukitsa makumi khumi, ndi maso a mbuye wanga mfumu achione; koma mbuye wanga mfumu alikukondwera bwanji ndi chinthu ichi? Koma mau a mfumu anapambana Yowabu ndi atsogoleri a khamulo. Ndipo Yowabu ndi atsogoleri a khamulo anatuluka pamaso pa mfumu kuti akawerenge anthu a Israele. Naoloka Yordani, namanga zithando ku Aroere ku dzanja lamanja kwa mudzi uli pakati pa chigwa cha Gadi, ndi ku Yazere; nafika ku Giliyadi ndi ku dera la Tatimuhodisi; nafika ku Dani-Yaana ndi kuzungulira, kufikira ku Sidoni, nafika ku linga la Tiro ndi kumidzi yonse ya Ahivi ndi ya Akanani; natulukira kumwera kwa Yuda ku Beereseba. Chomwecho pamene atayenda dziko lonse anafika ku Yerusalemu pakutha miyezi isanu ndi inai, ndi masiku makumi awiri. Ndipo Yowabu anapereka kwa mfumu kuchuluka kwa anthu adawawerenga; ndipo m'Israele munali anthu zikwi mazana asanu ndi atatu, ngwazi zosolola lupanga; ndi anthu a Yuda ndiwo zikwi mazana asanu. Pamenepo mtima wa Davide unamtsutsa, atatha kuwerenga anthuwo. Davide nati kwa Yehova, Ndinachimwa kwakukulu ndi chinthu chimene ndinachita; koma tsopano Yehova muchotse mphulupulu ya mnyamata wanu, pakuti ndinachita kopusa ndithu. Ndipo pouka Davide m'mawa mau a Yehova anafika kwa mneneri Gadi, mlauli wa Davide, kuti, Kalankhule ndi Davide, Atero Yehova, kuti, Ndikuikira zinthu zitatu; udzisankhire wekha chimodzi cha izo, ndikakuchitire chimenecho. Chomwecho Gadi anafika kwa Davide, namuuza nanena naye, Kodi zikugwereni m'dziko mwanu zaka zisanu ndi ziwiri za njala? Kapena muthawe adani anu akukupirikitsani miyezi itatu? Kapena m'dziko mwanu mukhale mliri masiku atatu? Chenjerani tsono ndi kulingalira bwino mau amene ine ndibwere nao kwa wonditumayo. Ndipo Davide ananena ndi Gadi, Ndipsinjika mtima kwambiri, tigwe m'dzanja la Yehova; pakuti zifundo zake nzazikulu; koma tisagwe m'dzanja la munthu. Chomwecho Yehova anatumiza mliri pa Israele kuyambira m'mawa kufikira nthawi yoikira; ndipo anafapo anthu zikwi makumi asanu ndi awiri kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba. Ndipo pamene mthenga anatambasulira dzanja lake ku Yerusalemu kuuononga, choipacho chinachititsa Yehova chisoni, Iye nauza mthenga wakuononga anthuwo, kuti, Kwafikira tsopano, bweza dzanja lako. Ndipo mthenga wa Yehova anali pa dwale la Arauna Myebusi. Ndipo Davide analankhula ndi Yehova pamene anaona mthenga wakudwalitsa anthu, nati, Onani ndachimwa ine, ndinachita mwamphulupulu; koma nkhosa izi zinachitanji? Dzanja lanu likhale pa ine ndi pa nyumba ya atate wanga. Ndipo Gadi anafika tsiku lomwelo kwa Davide nanena naye, Kwerani mukamangire Yehova guwa la nsembe pa dwale la Arauna Myebusi. Ndipo Davide anakwerako monga mwa kunena kwa Gadi, monga adalamulira Yehova. Ndipo Arauna anayang'ana naona mfumuyo ndi anyamata ake alikubwera kwa iye; natuluka Arauna naweramira pamaso pa mfumu nkhope yake pansi. Arauna nati, Mbuye wanga mfumu, mwadzeranji kwa mnyamata wanu? Ndipo Davide, anati, Kugula dwale lako ili, kuti ndimangirepo Yehova guwa lansembe, kuti mliriwo ulekeke kwa anthu. Arauna nati kwa Davide Mbuye wanga mfumu atenge napereke nsembe chomkomera; siizi ng'ombe za nsembe yopsereza, ndi zipangizo ndi zomangira ng'ombe zikhale nkhuni; zonsezi, mfumu, Arauna akupatsani mfumu. Ndipo Arauna anati kwa mfumu, Yehova Mulungu wanu akulandireni. Koma mfumu inati kwa Arauna, Iai; koma ndidzaligula kwa iwe pa mtengo wake, pakuti sindidzapereka kwa Yehova Mulungu wanga nsembe zopsereza zopanda mtengo wake. Momwemo Davide anagula dwalelo ndi ng'ombezo naperekapo masekeli makumi asanu a siliva. Ndipo Davide anamangirapo Yehova guwa la nsembe, napereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika. Momwemo Yehova anapembedzeka chifukwa cha dziko, ndi mliri wa pa Israele unalekeka. Ndipo mfumu Davide anakalamba nachuluka masiku ake; ndipo iwo anamfunda ndi zofunda, koma iye sanafundidwe. Pamenepo anyamata ake ananena naye, Amfunire mbuye wanga mfumu namwali, aimirire pamaso pa mfumu namsunge; nagone m'mfukato mwanu, kuti mbuye mfumu yanga afundidwe. Tsono anafunafuna m'malire monse a Israele namwali wokongola, napeza Abisagi wa ku Sunamu, nabwera naye kwa mfumu. Ndipo namwaliyo anali wokongola ndithu, namasunga mfumu namtumikira; koma mfumu sinamdziwa. Pamenepo Adoniya mwana wa Hagiti anadzikuza, nati, Ndikhala mfumu ndine; nadzikonzera agaleta ndi apakavalo ndi anthu makumi asanu omtsogolera mothamanga. Ndipo atate wake sadamvuta masiku ake onse, ndi kuti, Watero chifukwa ninji? Ndiponso anali munthu wokongola ndithu; napondana ndi Abisalomu. Ndipo anapangana ndi Yowabu mwana wa Zeruya, ndi Abiyatara wansembeyo; ndipo amenewo anamtsata Adoniya namthandiza. Koma Zadoki wansembe, ndi Benaya mwana wake wa Yehoyada, ndi Natani mneneri, ndi Simei, ndi Rei, ndi anthu amphamvu aja adali ndi Davide, sanali ndi Adoniya. Ndipo Adoniya anapha nkhosa ndi ng'ombe ndi nyama zonona pamwala pa Zoheleti, uli pafupi ndi chitsime cha Rogele, naitana abale ake onse ana a mfumu, ndi anthu onse a Yuda anyamata a mfumu; koma Natani mneneriyo, ndi Benaya, ndi anthu amphamvu aja, ndi Solomoni mbale wake, sanawaitane. Pamenepo Natani ananena ndi Bateseba amake wa Solomoni, nati, Kodi sunamva kuti Adoniya mwana wa Hagiti walowa ufumu, ndipo Davide mbuye wathu sadziwa? Ubwere tsono, ndikupangire, kuti usunge moyo wako, ndi moyo wa mwana wako Solomoni. Muka nulowe kwa mfumu Davide, nukati kwa iye, Mbuye wanga mfumu, kodi simunalumbirira mdzakazi wanu, ndi kuti, Zedi Solomoni mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wachifumu? Ndipo Adoniya akhaliranji mfumu? Taona, uli chilankhulire ndi mfumu, inenso ndidzalowa pambuyo pako, ndi kutsimikiza mau ako. Pamenepo Bateseba analowa kwa mfumu kuchipinda; ndipo mfumuyo inali yokalamba ndithu; ndipo Abisagi wa ku Sunamu anali kutumikira mfumu. Ndipo Bateseba anawerama nalambira mfumu, ndi mfumu niti, Ufunanji? Ndipo iye ananena nayo, Mbuye wanga, munalumbirira mdzakazi wanu pa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Zedi Solomoni mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wachifumu. Ndipo tsopano taonani, Adoniya walowa ufumu, ndipo inu mbuye wanga mfumu simudziwa. Ndipo iye anapha ng'ombe ndi nyama zonona ndi nkhosa zaunyinji, naitana ana amuna onse a mfumu, ndi Abiyatara wansembe, ndi Yowabu kazembe wa nkhondo; koma Solomoni mnyamata wanu sanamuitane. Ndipo tsopano, mbuye wanga mfumu, maso a Aisraele onse ali pa inu, kuti muwauze amene adzakhala pa mpando wachifumu wa mbuye wanga mfumu atamuka iye. Mukapanda kutero, kudzachitika, pamene mbuye wanga mfumu atagona kwa makolo ake, ine ndi mwana wanga Solomoni tidzayesedwa ochimwa. Ndipo taona, iye ali chilankhulire ndi mfumu, Natani mneneriyo analowamo. Ndipo anauza mfumu, kuti, Wafika Natani mneneriyo. Ndipo iye anafika pamaso pa mfumu, naweramitsa nkhope yake pansi pamaso pa mfumu. Ndipo Natani anati, Mbuye wanga mfumu, kodi inu munati, Adoniya adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala ndiye pa mpando wanga wachifumu? Popeza iye watsika lero, nakapha ng'ombe ndi nyama zonona ndi nkhosa zaunyinji, naitana ana amuna onse a mfumu, ndi akazembe a nkhondo, ndi Abiyatara wansembe; ndipo taonani, iwowo akudya ndi kumwa pamaso pake, nati, Akhale ndi moyo mfumu Adoniya. Koma ine, inde inedi mnyamata wanu, ndi Zadoki wansembe, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Solomoni mnyamata wanu, sanatiitane. Chinthu ichi chachitika ndi mbuye wanga mfumu kodi, ndipo simunadziwitsa mnyamata wanu amene adzakhala pa mpando wachifumu wa mbuye wanga mfumu atamuka iye? Tsono mfumu Davide anayankha, nati, Ndiitanireni Bateseba. Ndipo iye analowa pamaso pa mfumu, naima pamaso pa mfumu. Ndipo mfumu inalumbira, niti, Pali Yehova amene anapulumutsa moyo wanga m'nsautso monse, zedi monga umo ndinalumbirira iwe pa Yehova Mulungu wa Israele, ndi kuti, Zoonadi Solomoni mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wachifumu m'malo mwa ine, zedi nditero lero lomwe. Pamenepo Bateseba anaweramitsa pansi nkhope yake, nalambira mfumu, nati, Mbuye wanga mfumu Davide akhale ndi moyo nthawi zamuyaya. Ndipo mfumu Davide anati, Kandiitanireni Zadoki wansembeyo, ndi Natani mneneriyo, ndi Benaya mwana wa Yehoyada. Iwo nalowa pamaso pa mfumu. Ndipo mfumu inati kwa iwo, Tengani akapolo a mfumu yanu, nimukweze Solomoni mwana wanga pa nyuru yangayanga, nimutsikire naye ku Gihoni. Ndipo Zadoki wansembe ndi Natani mneneri akamdzoze kumeneko akhale mfumu ya Israele; ndipo muombe lipenga, ndi kuti, Mfumu Solomoni akhale ndi moyo. Pamenepo mumtsate iye, iye nadzadza nadzakhala pa mpando wanga wachifumu, popeza adzakhala iyeyu mfumu m'malo mwanga; ndipo ndamuika iye akhale mtsogoleri wa Israele ndi Yuda. Ndipo Benaya mwana wa Yehoyada anayankha mfumu, nati, Amen, ateronso Yehova Mulungu wa mbuye wanga mfumu. Monga umo Yehova anakhalira ndi mbuye wanga mfumu momwemo akhalenso ndi Solomoni, nakuze mpando wake wachifumu upose mpando wachifumu wa mbuye wanga mfumu Davide. Pamenepo Zadoki wansembe, ndi Natani mneneri, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Akereti, ndi Apeleti aja anatsika, nakweza Solomoni pa nyuru ya mfumu Davide, nafika naye ku Gihoni. Ndipo Zadoki wansembe anatenga nyanga ya mafuta inali m'Chihema, namdzoza Solomoni. Ndipo iwo anaomba lipenga, ndi anthu onse anati, Mfumu Solomoni akhale ndi moyo. Ndipo anthu onse anakwera namtsata, naliza zitoliro, nakondwera ndi kukondwera kwakukulu, kotero kuti pansi panang'ambika ndi phokoso lao. Ndipo Adoniya ndi oitanidwa onse anali ndi iye analimva atatha kudya. Ndipo Yowabu, pakumva kuomba kwa lipengalo, anati, Phokosolo ndi chiyani kuti m'mudzi muli chibumo? Iye akali chilankhulire, taona, walowa Yonatani mwana wa Abiyatara wansembe, ndipo Adoniya anati, Lowa, popeza ndiwe munthu wamphamvu, nubwera nao uthenga wabwino. Ndipo Yonatani anayankha, nati kwa Adoniya, Zedi Davide mbuye wathu mfumu walonga Solomoni ufumu: ndipo mfumu yatumanso Zadoki wansembe, ndi Natani mneneri, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Akereti, ndi Apeleti aja, namkweza iye pa nyuru ya mfumu. Ndipo Zadoki wansembe ndi Natani mneneri anamdzoza mfumu ku Gihoni, ndipo achokera kumeneko chikondwerere, ndi m'mudzimo muli phokoso. Ndilo phokoso limene mwamvali. Ndiponso Solomoni wakhala pa chimpando cha ufumu. Ndiponso akapolo a mfumu anadzadalitsa Davide mbuye wathu mfumu, nati, Mulungu wanu aposetse dzina la Solomoni lipunde dzina lanu, nakulitse mpando wake wachifumu upose mpando wanu wachifumu; ndipo mfumu anawerama pakamapo. Ndiponso watero mfumu, Wolemekezeka Yehova Mulungu wa Israele, amene wapereka lero wina wokhala pa mpando wanga wachifumu, maso anga ali chipenyere. Pamenepo oitanidwa onse a Adoniya anachita mantha, nanyamuka, napita yense njira yake. Ndipo Adoniya anaopa chifukwa cha Solomoni, nanyamuka, nakagwira nyanga za guwa la nsembe. Ndipo anthu anakauza Solomoni, kuti, Taonani, Adoniya aopa mfumu Solomoni, popeza taonani, wagwira nyanga za guwa la nsembe, nati, Mfumu Solomoni alumbirire ine lero kuti sadzandipha kapolo wake ndi lupanga. Ndipo Solomoni anati, Iye akakhala munthu woyenera silidzagwa pansi tsitsi lake limodzi lonse; koma mukapezeka mwa iye choipa, adzafadi. Tsono mfumu Solomoni anatuma anthu nakamtsitsa ku guwa la nsembe. Iye nadza, nagwadira mfumu Solomoni; Solomoni nati kwa iye, Pita kwanu. Pakuyandikira masiku ake a Davide akuti amwalire, analamulira Solomoni mwana wake, nati, Ndimuka ine njira ya dziko lonse: limba mtima tsono, nudzionetse umunthu; nusunge chilangizo cha Yehova Mulungu wako, kuyenda m'njira zake, kusunga malemba ndi malamulo ndi maweruzo ndi umboni wake, monga mulembedwa m'chilamulo cha Mose, kuti ukachite mwa nzeru m'zonse ukachitazo, ndi kumene konse ukatembenukirako; kuti Yehova akakhazikitse mau ake adanenawo za ine, kuti, Ngati ana ako akasunga bwino njira zao, kuyenda moona pamaso pa Ine ndi mtima wao wonse ndi moyo wao wonse, nditi sipadzakusowa mwamuna mmodzi pa mpando wachifumu wa Israele. Ndiponso udziwa chimene Yowabu mwana wa Zeruya anandichitira, inde chimene anawachitira akazembe awiri aja a magulu a nkhondo a Israele, ndiwo Abinere mwana wa Nere, ndi Amasa mwana wa Yetere, amene aja anawapha, nakhetsa mwazi ngati wa nkhondo masiku a mtendere, napaka mwazi wa nkhondo pa lamba lake la m'chuuno mwake, ndi pa nsapato za pa mapazi ake. Chita mwa nzeru yako tsono, osalola mutu wake waimvi utsikire kumanda ndi mtendere. Koma uchitire zokoma ana amuna aja a Barizilai wa ku Giliyadi, akhale pakati pa akudyera pa gome lako, popeza momwemo amenewo anandiyandikira muja ndinalikuthawa Abisalomu mbale wako. Ndipo taona uli naye Simei mwana wa Gera wa fuko la Benjamini wa ku Bahurimu, yemwe uja adanditemberera ndi temberero lalikulu tsiku lija lakupita ine ku Mahanaimu; koma anadzakomana ndi ine pa Yordani, ndipo ndinalumbirira iye pa Yehova, kuti, Sindikupha iwe ndi lupanga. Ndipo tsono, usamuyesera iye wosachimwa, popeza ndiwe munthu wanzeru, ndipo udziwa umo uyenera kumchitira iye, nutsitsire mutu wake waimvi ndi mwazi kumanda. Ndipo Davide anagona pamodzi ndi makolo ake, naikidwa m'mudzi wa Davide. Ndipo masiku ake akukhala Davide mfumu ya Israele anali zaka makumi anai; zaka zisanu ndi ziwiri anakhala mfumu ku Hebroni, ndi zaka makumi atatu mphambu chitatu anakhala mfumu ku Yerusalemu. Tsono Solomoni anakhala pa mpando wachifumu wa Davide atate wake, ndipo ufumu wake unakhazikika kwakukulu. Pomwepo Adoniya mwana wa Hagiti anadza kwa Bateseba amai wake wa Solomoni, ndipo mkaziyo anati, Kodi wadza ndi mtendere? Nati, Ndi mtendere umene. Anatinso, Ndili nanu mau. Nati iye, Tanena. Nati iye, Mudziwa kuti ufumu unali wanga, ndi kuti Aisraele onse anaika maso ao pa ine, kuti ndikhale mfumu ndine; koma ufumu watembenuka nukhala wa mbale wanga, popeza iye anaulandira kwa Yehova. Ndipo tsopano, ndikupemphani pempho limodzi, musandikaniza. Ndipo mkaziyo anati kwa iye, Tanena. Nati iye, Mundinenere kwa mfumu Solomoni, popeza sakukanizani, kuti andipatse Abisagi wa ku Sunamu akhale mkazi wanga. Ndipo Bateseba anati, Chabwino, ndidzakunenera kwa mfumu. Tsono Bateseba ananka kwa mfumu Solomoni kukanenera Adoniya kwa iye. Ndipo mfumu inanyamuka kukomana naye, namuweramira nakhalanso pa mpando wake wachifumu, naikitsa mpando wina wa amake wa mfumu, nakhala iye ku dzanja lake lamanja. Pamenepo mkaziyo anati, Ndikupemphani kapempho kamodzi, musandikaniza. Ndipo mfumu inati kwa iye, Tapemphani amai wanga, popeza sindikukanizani. Ndipo iye anati, Abisagi wa ku Sunamu apatsidwe kwa Adoniya mbale wanu akhale mkazi wake. Ndipo mfumu Solomoni anayankha, nati kwa amai wake, Mupempheranji Abisagi wa ku Sunamu akhale wake wa Adoniya? Mumpempherenso ufumu, popeza ndiye mkulu wanga; inde ukhale wake, ndi wa Abiyatara wansembeyo, ndi wa Yowabu mwana wa Zeruya. Pomwepo mfumu Solomoni analumbira pa Yehova, nati, Mulungu andilange naonjezepo, zedi Adoniya wadziphetsa yekha ndi mau awa. Ndipo tsono, pali Yehova amene wandikhazikitsa ine, nandikhalitsa pampando wachifumu wa Davide atate wanga, nandimangira nyumba monga analonjeza, zedi Adoniya aphedwa lero lomwe. Ndipo mfumu Solomoni anatuma dzanja la Benaya mwana wa Yehoyada, ndipo anamgwera, namwalira iye. Ndipo mfumu inanena ndi Abiyatara wansembeyo, Pita ku Anatoti ku minda yako; pakuti wakutidwa ndi imfa; koma sindikupha iwe lero lino, chifukwa unanyamula likasa la Ambuye Yehova pamaso pa Davide atate wanga, ndi popeza unanzunzidwa monse umo atate wanga Davide anazunzidwamo. Motero Solomoni anachotsa Abiyatara asakhalenso wansembe wa Yehova, kuti akakwaniritse mau a Yehova amene aja adalankhula ku Silo za mbumba ya Eli. Ndipo mbiriyi inamfika Yowabu, pakuti Yowabu anapatukira kwa Adoniya, angakhale sanapatukire kwa Abisalomu. Ndipo Yowabu anathawira ku chihema cha Yehova, nagwira nyanga za guwa la nsembe. Ndipo anamuuza mfumu Solomoni, kuti, Yowabu wathawira ku chihema cha Yehova; ndipo taonani, wakhala ku guwa la nsembe. Pomwepo Solomoni anatuma Benaya mwana wa Yehoyada, nati, Kamkwere. Nafika Benaya ku chihema cha Yehova, nati kwa iye, Mfumu itero, Tatuluka. Nati, Iai, koma ndifere pompano. Ndipo Benaya anabweza mau kwa mfumu, nati, Yowabu wanena chakuti, nandiyankha mwakutimwakuti. Ndipo mfumu inati kwa iye, Chita monga umo wanena iye, numkwere, numuike; kuti undichotsere ine ndi nyumba ya atate wanga mwazi uja Yowabu anaukhetsa wopanda chifukwa. Ndipo Yehova adzambwezera mwazi wake pa mutu wake wa iye yekha, popeza iye anawakantha anthu awiri olungama ndi okoma oposa iye mwini, nawapha ndi lupanga, atate wanga Davide osadziwa, ndiwo Abinere mwana wa Nere kazembe wa khamu la nkhondo la Israele, ndi Amasa mwana wa Yetere kazembe wa khamu la nkhondo la Yuda. Motero mwazi wao udzabweranso pa mutu wake wa Yowabu, ndi pa mutu wa mbumba yake, ku nthawi yamuyaya; koma Davide, ndi mbumba yake, ndi banja lake, ndi mpando wake wachifumu adzakhala ndi mtendere wa Yehova ku nthawi yamuyaya. Pomwepo Benaya mwana wa Yehoyada anakwera namkantha iye, namupha; ndipo anaikidwa m'nyumba yakeyake kuchipululu. Ndipo mfumu inaika Benaya mwana wa Yehoyada m'malo mwake kutsogolera khamu la nkhondo, ndi mfumu inaika Zadoki wansembe m'malo mwa Abiyatara. Ndipo mfumu inatuma munthu kukaitana Simei, nati kwa iye, Udzimangire nyumba m'Yerusalemu, nukhale komweko osatulukako kunka kwina konse. Popeza tsiku lomwelo lakutuluka iwe ndi kuoloka mtsinje Kidroni, tadziwa ndithu kuti udzafadi, mwazi wako udzakhala pa mutu wa iwe wekha. Ndipo Simei anena ndi mfumu, Mau awa ndi abwino; monga momwe mwanena mbuye wanga mfumu momwemo ndidzachita kapolo wanu. Ndipo Simei anakhala m'Yerusalemu masiku ambiri. Ndipo kunachitika, zitapita zaka zitatu, kuti akapolo awiri a Simei anathawira kwa Akisi mwana wa Maaka mfumu ya Gati. Ndipo anamuuza Simei, nati, Taonani, akapolo anu akhala ku Gati. Ndipo Simei ananyamuka, namangirira mbereko pa bulu wake, namka ku Gati kwa Akisi kukafuna akapolo ake; namuka Simei, nabwera nao akapolo ake kuchokera ku Gati. Ndipo anamuuza Solomoni, kuti, Simei wachoka ku Yerusalemu kunka ku Gati, nabweranso. Ndipo mfumu inatuma munthu kukaitana Simei, niti kwa iye, Kodi sindinakulumbiritsa pa Yehova ndi kukuchenjeza, kuti, Tadziwa ndithu, kuti tsiku lakutuluka iwe ndi kukayenda kwina konse udzafa ndithu? Ndipo iwe unati kwa ine, Mau amene ndawamva ndi abwino. Sunasunga chifukwa ninji lumbiro la pa Yehova, ndi lamulo lija ndinakulamulira iwe? Tsono mfumu inanenanso ndi Simei Udziwa iwe choipa chonse mtima wako umadziwacho, chimene udachitira Davide atate wanga; chifukwa chake Yehova adzakubwezera choipa chako pamutu pako mwini. Koma mfumu Solomoni adzadalitsika, ndi mpando wachifumu wa Davide udzakhazikika pamaso pa Yehova ku nthawi yamuyaya. Pamenepo mfumu inalamulira Benaya mwana wa Yehoyada, ndipo iye anatuluka namkwera, namwalira iye. Ndipo ufumu unakhazikika m'dzanja la Solomoni. Ndipo Solomoni anapalana ubwenzi ndi Farao mfumu ya Aejipito, natenga mwana wamkazi wa Farao, nadza naye kumudzi wa Davide, mpaka atamanga nyumba ya iye yekha, ndi nyumba ya Yehova, ndi linga lozinga Yerusalemu. Koma anthu anaphera nsembe pamisanje, popeza panalibe nyumba yomangira dzina la Yehova kufikira masiku omwewo. Ndipo Solomoni anakondana ndi Yehova, nayenda m'malemba a Davide atate wake; koma anaphera nsembe nafukiza zonunkhira pamisanje. Ndipo mfumu inapita ku Gibiyoni kukaphera nsembe kumeneko; popeza msanje waukulu unali kumeneko, Solomoni anapereka nsembe zopsereza chikwi chimodzi pa guwalo la nsembe. Ku Gibiyoni Yehova anaonekera Solomoni m'kulota usiku, nati Mulungu, Tapempha chimene ndikupatse. Ndipo Solomoni anati, Munamchitira mtumiki wanu Davide atate wanga zokoma zazikulu, monga umo anayenda pamaso panu ndi choonadi ndi chilungamo ndi mtima woongoka ndi Inu; ndipo mwamsungira chokoma ichi chachikulu kuti mwampatsa mwana kukhala pa mpando wake wachifumu monga lero lino. Ndipo tsopano, Yehova Inu Mulungu wanga, mwalonga ine kapolo wanu ufumu m'malo mwa atate wanga Davide, koma ine ndine kamwana, sindidziwa kutuluka kapena kulowa. Ndipo kapolo wanu ndili pakati pa anthu anu amene Inu munawasankha, anthu ambirimbiri osawerengeka, kapena kulembeka m'unyinji wao. Patsani tsono kapolo wanu mtima womvera wakuweruza anthu anu; kuti ndizindikire pakati pa zabwino ndi zoipa; pakuti akutha ndani kuweruza anthu anu ambiri amene? Ndipo mau amenewa anakondweretsa Yehova kuti Solomoni anapempha chimenechi. Ndipo Mulungu anati kwa iye, Popeza wapempha chimenechi, osadzipemphera masiku ambiri, osadzipempheranso chuma, osadzipempheranso moyo wa adani ako, koma wadzipemphera nzeru zakumvera milandu; taona, ndachita monga mwa mau ako; taona ndakupatsa mtima wanzeru ndi wakuzindikira, kotero kuti panalibe wina wolingana ndi iwe kale, ndipo sadzakhalanso wina wolingana ndi iwe utamuka. Ndiponso zimene sunazipempha adakupatsa, ndipo chuma ndi ulemu, kuti pakati pa mafumu sipadzakhala ina yolingana ndi iwe masiku ako onse. Ndipo ukadzayenda m'njira zanga kusunga malemba anga ndi malamulo anga, monga atate wako Davide anayendamo, Ine ndidzachulukitsa masiku ako. Ndipo Solomoni anauka, ndipo taona, ndilo loto; nabwera ku Yerusalemu, naima ku likasa la chipangano cha Yehova, napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zamtendere, nakonzera anyamata ake onse madyerero. Pamenepo analowa kwa mfumu akazi awiri, ndiwo adama, naima pamaso pake. Ndipo mkazi mmodzi anati, Mbuye wanga, ine ndi mkazi uyu tikhala awiri m'nyumba imodzi; ndipo ine ndinaona mwana, iye ali m'nyumbamo. Ndipo kunachitika kuti tsiku lachitatu nditaona ine mwana, mnzangayu anaonanso mwana; ndipo ife tinali pamodzi, munalibe mlendo ndi ife m'nyumbamo, koma ife awiri m'nyumbamo. Ndipo mwana wa mnzangayu anamwalira usiku, pokhala iyeyu anamgonera. Ndipo iye anauka pakati pa usiku, natenga mwana wanga kumimba kwanga, mdzakazi wanu ndili m'tulo, namuika m'mfukato mwake, naika mwana wake wakufa m'mfukato mwanga. Ndipo pouka ine m'mawa kuyamwitsa mwana wanga ndaona, ngwakufa, koma nditamzindikira m'mawa ndaona si mwana wanga wobala ine ai. Ndipo mkazi winayo anati, Iai, koma wamoyoyu ndi mwana wanga, ndi wakufayu ndi mwana wako. Ndipo uja anati, Iai, koma wakufayu ndi mwana wako, ndi wamoyoyu ndi mwana wanga. Motero iwo analankhula pamaso pa mfumu. Tsono mfumu inati, Uyu akuti, Wamoyoyu ndiye mwana wanga ndi wakufayu ndiye mwana wako; ndipo winayo akuti, Iai, koma mwana wako ndiye wakufayu, ndi mwana wanga ndiye wamoyoyu. Niti mfumu, Kanditengereni chimpeni. Ndipo iwo anabwera ndi chimpeni kwa mfumu. Mfumu niti, Dula pakati mwana wamoyoyu, nupatse mmodzi chipinjiri, ndi wina chipinjiri chake. Koma mkazi amene mwana wamoyo anali wake analankhula ndi mfumu, popeza mtima wake unalira mwana wake, nati, Ha? Mbuye wanga, mumpatse uyo mwana wamoyo osamupha konse. Koma winayo anati, Asakhale wanga kapena wako, dulani. Pamenepo mfumu inayankha, niti, Mumpatse wachifundoyo mwana wamoyo, osamupha konse, uyo ndiye amake. Ndipo Aisraele onse anamva maweruzidwe ake idaweruza mfumu, naopa mfumu; pokhala anaona kuti nzeru ya Mulungu inali mwa iye yakuweruza. Ndipo mfumu Solomoni anali mfumu ya Israele yense. Ndipo akulu a mfumu ndi awa: Azariya mwana wa Zadoki anali wansembe, Elihorefe ndi Ahiya ana a Sisa alembi, Yehosafati mwana wa Ahiludi wolembera mbiri, ndi Benaya mwana wa Yehoyada anali kazembe wa nkhondo, ndi Zadoki ndi Abiyatara anali ansembe, ndi Azariya mwana wa Natani anayang'anira akapitao, ndipo Zabudi mwana wa Natani anali wansembe ndi nduna yopangira mfumu, ndi Ahisara Adoniramu mwana wa Abida anali wamsonkho. Ndipo Solomoni anali nao akapitao khumi ndi awiri akuyang'anira Aisraele onse, akufikitsira mfumu ndi banja lake zakudya; aliyense anafikitsa zakudya zofikira mwezi umodzi wa chaka. Ndipo maina ao ndiwo: Benihuri anatengetsa ku mapiri a Efuremu; Benedekere ku Makazi ndi Saalibimu ndi Betesemesi ndi Elonibetehanani; Benihesedi ku Aruboti ndi Soko ndi dziko lonse la Hefere; Benabinadabu ku mtunda wa Dori, mkazi wake ndiye Tafati mwana wa Solomoni; Baana mwana wa Ahiludi ku Taanaki ndi Megido ndi Beteseani konse, ali pafupi ndi Zaretani kunsi kwa Yezireele, kuyambira ku Beteseani kufikira ku Abele-Mehola, kufikiranso kundunji ku Yokomeamu; Benigebere ku Ramoti Giliyadi, iyeyo anali nayo midzi ya Yairi mwana wa Manase ili m'Giliyadiyo, iye anali nalo dziko la Arigobu lili m'Basani, midzi yaikulu makumi asanu ndi limodzi yamalinga ndi zitseko zamkuwa; Ahinadabu mwana wa Ido ku Mahanaimu; Ahimaazi ku Nafutali, iyeyu adakwatira Basemati mwana wa Solomoni; Baana mwana wa Husai ku Asere ndi ku Bealoti; Yehosafati mwana wa Paruwa ku Isakara; Simei mwana wa Ela ku Benjamini; Gebere mwana wa Uri ku dziko la Giliyadi, dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, ndi la Ogi mfumu ya Basani; munalibe kapitao wina m'deramo. Ayuda ndi Aisraele anachuluka ngati mchenga wa kunyanja, namadya namamwa namakondwera. Ndipo Solomoni analamulira maiko onse, kuyambira ku Yufurate kufikira ku dziko la Afilisti ndi ku malire a Ejipito; anthu anabwera nayo mitulo namtumikira Solomoni masiku onse a moyo wake. Ndipo zakudya za Solomoni zofikira tsiku limodzi zinali miyeso makumi atatu ya ufa wosalala, ndi miyeso makumi asanu ndi limodzi ya ufa wamankhupete, ng'ombe zonenepa khumi, ndi ng'ombe za kubusa makumi awiri, ndi nkhosa zana limodzi, osawerenganso ngondo ndi nswala ndi mphoyo ndi mbalame zoweta. Pakuti analamulira dziko lonse lili tsidya lino la Yufurate, kuyambira ku Tifisa kufikira ku Gaza, inde mafumu onse a ku tsidya lino la Yufurate; nakhala ndi mtendere kozungulira konseko. Ndipo Ayuda ndi Aisraele anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pa mpesa wake ndi mkuyu wake, kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba, masiku onse a Solomoni. Ndipo Solomoni anali nazo zipinda za akavalo a magaleta ake zikwi khumi mphambu ziwiri. Ndipo akapitao aja anatengetsera chakudya Solomoni ndi anthu onse akudya ku gome la mfumu Solomoni, munthu yense m'mwezi mwake, sanalole kanthu kasoweke. Barelenso ndi udzu wa akavalo ndi ngamira anabwera nazo kumalo kwao, munthu yense monga momwe anamuuzira. Ndipo Mulungu anampatsa Solomoni nzeru ndi luntha lambiri, ndi mtima wodziwa za mitundumitundu, zonga mchenga uli m'mphepete mwa nyanja. Ndipo nzeru ya Solomoni inaposa nzeru za anthu onse akum'mawa, ndi nzeru zonse za ku Ejipito. Pakuti anali wanzeru woposa anthu onse, woposa Etani wa ku Ezara, ndi Hemani, ndi Kalikoli, ndi Darida ana a Maholi; ndipo mbiri yake inafikira amitundu onse ozungulira. Ndipo ananena miyambo zikwi zitatu, ndipo nyimbo zake zinali chikwi chimodzi mphambu zisanu. Nakamba za mitengo, kuyambira mkungudza uli ku Lebanoni kufikira hisope wophuka pakhoma; anakambanso za nyama ndi mbalame ndi zinthu zokwawa pansi ndi za nsomba. Ndipo anafikapo anthu a mitundu yonse kudzamva nzeru ya Solomoni, ochokera kwa mafumu onse a dziko lonse lapansi, amene adamva mbiri ya nzeru yake. Ndipo Hiramu mfumu ya ku Tiro anatuma anyamata ake kwa Solomoni, popeza anamva kuti adamdzoza mfumu m'malo mwa atate wake; pakuti Hiramu adakondana ndi Davide masiku onse. Ndipo Solomoni anatumiza mau kwa Hiramu, nati, Mudziwa inu kuti atate wanga Davide sanathe kumangira dzina la Yehova Mulungu wake nyumba, chifukwa cha nkhondo zakumzinga konseko, mpaka atawaika Yehova pansi pa mapazi ake. Koma tsopano Yehova Mulungu wanga wandipumulitsa ku mbali zonse; palibe wotsutsana nane, kapena choipa chondigwera. Ndipo taonani, ndikuti ndimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, monga Yehova anauza atate wanga Davide, ndi kuti, Mwana wako ndidzamuika pa mpando wako wachifumu m'malo mwako, iyeyo adzamangira dzina langa nyumbayo. Ndipo tsono, lamulirani kuti anditemere mitengo yamkungudza ku Lebanoni, ndipo akapolo anga adzakhala ndi akapolo anu, ndipo ndidzakupatsani mphotho ya akapolo anu monga mudzanena; popeza mudziwa kuti pakati pa ife palibe mmisiri wakudziwa kutema mitengo ngati anthu a ku Sidoni. Ndipo kunachitika, pamene Hiramu anamva mau ake a Solomoni, anakondwera kwakukulu, nati, Alemekezeke Yehova lero amene wampatsa Davide mwana wanzeru akhale mfumu ya anthu aunyinji amenewa. Ndipo Hiramu anatumiza kwa Solomoni, nati, Ndazimva zija munatumiza kwa inezo, ndidzachita chifuniro chanu chonse, kunena za mitengo yamkungudza ndi mitengo yamlombwa. Akapolo anga adzatsika nayo ku Lebanoni kufika nayo ku nyanja, ndipo ine ndidzaiyandamitsa paphaka kufikira komwe mudzandiuzako, ndi kumeneko ndidzaimasula, ndipo mudzaitenga; nimudzachita chifuniro changa, kumapatsa banja langa zakudya. Tsono Hiramu anapatsa Solomoni mitengo yamkungudza ndi mitengo yamlombwa monga momwe anafuniramo. Ndipo Solomoni anapatsa Hiramu miyeso ya tirigu zikwi makumi awiri ndiyo zakudya za banja lake, ndi miyeso makumi awiri ya mafuta oyera; motero Solomoni anapatsa Hiramu chaka ndi chaka. Ndipo Yehova anapatsa Solomoni nzeru monga momwe adamlonjezera; ndipo panali mtendere pakati pa Hiramu ndi Solomoni, iwo awiri napangana pamodzi. Ndipo mfumu Solomoni anasonkhetsa athangata mwa Aisraele onse, ndi athangatawo ndiwo anthu zikwi makumi atatu. Ndipo anawatuma ku Lebanoni mwezi umodzi zikwi khumi kuwasintha, mwezi umodzi iwo anali ku Lebanoni, miyezi iwiri anali kwao; ndipo Adoniramu anali kapitao wa athangata. Ndipo Solomoni anawasenzetsa akatundu anthu zikwi makumi asanu ndi awiri, ndi anthu zikwi makumi asanu ndi atatu anatema m'mapiri; osawerenga akapitao a Solomoni akuyang'anira ntchito, ndiwo zikwi zitatu mphambu mazana atatu, amenewo analamulira anthu aja akugwira ntchito. Ndipo mfumu inalamula iwo, natuta miyala yaikuluikulu ya mtengo wapatali, kuika maziko ake a nyumbayo ndi miyala yosemasema. Ndipo omanga nyumba a Solomoni ndi omanga nyumba a Hiramu ndi anthu a ku Gebala anaisema, naikonza mitengo ndi miyala yakumangira nyumbayo. Ndipo kunachitika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi asanu ndi atatu atatuluka ana a Israele m'dziko la Ejipito, chaka chachinai chakukhala Solomoni mfumu ya Israele, m'mwezi wa Zivi, ndiwo mwezi wachiwiri, iye anayamba kumanga nyumba ya Yehova. Ndipo nyumbayo mfumu Solomoni anaimangira Yehova, m'litali mwake munali mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi m'mimba mwake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake mikono makumi atatu. Ndipo anamanga chipinda cholowera pakhomo pa nyumba ya Kachisiyo, m'litali mwake munali mikono makumi awiri monga m'mimba mwake mwa nyumbayo, kupingasa kwake kunali mikono khumi ku khomo la nyumba. Ndipo m'nyumbamo anamanga mazenera a sefa wokhazikika. Ndipo anamanga zipinda zosanjikizana zogundana ndi khoma, kuzungulira makoma a nyumba ya Kachisi, ndi chipinda chamkati; namanga zipinda zozinga. Chipinda chapansicho kupingasa kwake kunali mikono isanu, chapakaticho kupingasa kwake mikono isanu ndi umodzi, chachitatucho kupingasa kwake mikono isanu ndi iwiri; pakuti kubwalo anachepsa khoma pozungulirapo, mitanda isalongedwe m'makoma a nyumba. Ndipo nyumbayo pomangidwa inamangidwa ndi miyala yokonzeratu asanaitute; ndipo m'nyumbamo simunamveka kulira nyundo, kapena nkhwangwa, kapena chipangizo chachitsulo, pomangidwa iyo. Khomo lolowera m'zipinda za pakati linali ku mbali ya ku dzanja lamanja ya nyumba; ndipo anthu amakwerera pa makwerero ozunguniza, kufikira ku zipinda za pakati, ndi kutuluka m'zapakatizo kulowa m'zachitatuzo. Momwemo anamanga nyumbayo naitsiriza, naika mitanda, naifolera ndi matabwa amikungudza. Ndipo anamanga zipindazo zogundana ndi nyumba yonseyo, chipinda chilichonse msinkhu wake mikono isanu; ndipo anazilumikizitsa kunyumba ndi mitengo yamkungudza. Ndipo mau a Yehova anafika kwa Solomoni, nati, Kunena za nyumba yino ulikuimanga, ukamayenda iwe m'malemba anga, ndi kumachita maweruzo anga, ndi kumasunga malamulo anga onse kuyendamo, pamenepo Ine ndidzakhazikitsira iwe mau anga amene ndinauza Davide atate wako. Ndipo ndidzakhala pakati pa ana a Israele osawasiya anthu anga a Israele. Tsono Solomoni anamanga nyumbayo naitsiriza. Ndipo anatchinga makoma a nyumba m'katimo ndi matabwa amkungudza, kuyambira pansi kufikira posanja, natchinga m'katimo ndi matabwa, nayala pansi m'nyumbamo matabwa amlombwa. Ndipo anadulitsa ndi matabwa amkungudza mikono makumi awiri m'kati mwa nyumba m'tsogolo mwake, kuyambira pansi kulekeza kumitanda; ichi anamanga kukhala chipinda chamkati, malo opatulika kwambiri. Ndipo nyumbayo, ndiyo Kachisi wa kutsogolo kwa chipindacho, inali ya mikono makumi anai. Ndipo m'kati mwa nyumba munali mikungudza yosemasema, ngati zikho ndi maluwa oti gada; munali mikungudza yokhayokha simunaoneka mwala ai. Ndipo anakonza m'kati mwa nyumba m'tsogolo mwake, kuikamo likasa la chipangano la Yehova. Ndipo m'kati mwa chipindacho, m'litali mwake munali mikono makumi awiri, kupingasa kwake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake mikono makumi awiri, kupingasa kwake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake mikono makumi awiri; ndipo anamukuta ndi golide wayengetsa, nakutanso guwa la nsembe ndi matabwa amkungudza. Momwemo Solomoni anakuta m'kati mwa nyumba ndi golide woyengetsa, natambalika maunyolo agolide chakuno cha chipinda chamkati, namukuta ndi golide. Ndipo nyumba yonse anaikuta ndi golide mpaka adatha nyumba yonse, ndi guwa lonse la nsembe linali chakuno cha chipinda chamkati analikuta ndi golide. Ndipo m'chipinda chamkatimo anasema mitengo ya azitona akerubi awiri, yense wa msinkhu wake mikono khumi. Ndipo phiko limodzi la kerubi linali la mikono isanu, ndi phiko lina la kerubi linalinso la mikono isanu; kuyambira ku nsonga ya phiko limodzi kufikira ku nsonga ya phiko lina inali mikono khumi. Ndi kerubi winayo msinkhu wake unali mikono khumi; akerubi onse awiri anafanana muyeso wao ndi msinkhu wao. Msinkhu wa kerubi mmodzi unali mikono khumi, ndi wa kerubi wina momwemo. Ndipo anaika akerubiwo m'chipinda cha m'katimo, ndi mapiko a akerubiwo anatambasuka kotero kuti phiko lake la kerubi mmodzi linajima ku khoma limodzi, ndipo phiko la kerubi wina linajima khoma lina, ndi mapiko ao anagundana pakati pa nyumba. Ndipo anawakuta akerubi ndi golide. Nalemba m'makoma onse akuzinga chipinda mafano olemba ngati akerubi ndi migwalangwa ndi maluwa oti gada, m'katimo ndi kumbuyo kwake. Ndipo anakuta ndi golide pansi pake pa nyumba m'katimo ndi kunja. Ndipo pa khomo la chipinda chamkati anapanga zitseko za mtengo wa azitona, chitando cha khomolo chinali limodzi la magawo asanu a khoma lake. Zitseko ziwiri zomwe zinali za mtengo wa azitona, anasemapo ngati akerubi ndi migwalangwa ndi maluwa oti gada, nawakuta ndi golide; inde anakutanso ndi golide akerubi ndi migwalangwayo. Momwemo anapanganso mphuthu za azitona za pa khomo la Kachisi, chitando chake chinali limodzi la magawo anai a khoma; ndi zitseko ziwiri za mitengo yamlombwa pa khomo lina; panali chitseko chopatukana, ndi pa linzake panali chitseko chopatukana. Ndipo analembapo ngati akerubi ndi migwalangwa ndi maluwa oti gada, nakuta zolembazo ndi golide wopsapsala. Ndipo bwalo la m'kati analimanga mizere itatu ya miyala yosemasema, ndi mzere umodzi wa mitanda yamkungudza. Maziko ake a nyumba ya Yehova anaikidwa m'chaka chachinai m'mwezi wa Zivi. Ndipo m'chaka chakhumi ndi chimodzi m'mwezi wa Buli ndiwo mwezi wachisanu ndi chitatu anatsiriza nyumba konsekonse monga mwa mamangidwe ake onse. Momwemo anaimanga zaka zisanu ndi ziwiri. Koma nyumba ya iye yekha Solomoni anaimanga zaka khumi mphambu zitatu, natsiriza nyumba yake yonse. Anamanganso nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni, m'litali mwake munali mikono zana limodzi, kupingasa kwake mikono makumi asanu, ndi msinkhu wake mikono makumi atatu; naisanja pa mizere inai ya mapanda amkungudza, ndi mitanda yamkungudza, ndi mitanda yamkungudza yotanthalika mapandawo. Ndipo inayalidwa ndi mkungudza pamwamba pa zipinda makumi anai mphambu zisanu zolongosoledwa pa mapanda, mzere umodzi zipinda khumi mphambu asanu. Ndipo panali mazenera m'mizere itatuyo, zenera limodzi lopenyana ndi linzake mizere itatu. Ndipo makomo onse ndi mphuthu zonse zinali zaphwamphwa maonekedwe ake, ndipo zenera limodzi linapenyana ndi linzake mizere itatu. Ndipo anamanga khonde la nsanamira, m'litali mwake munali mikono makumi asanu, kupingasa kwake mikono makumi atatu; ndipo panali khonde lina patsogolo pake, ndi nsanamira ndi mitanda patsogolo pakepo. Ndipo anamanga khonde la mpando wachifumu loweruziramo iye, ndilo khonde la milandu, ndipo linayalidwa ndi mkungudza pansi ndi posanja. Ndipo nyumba yake yakukhalamo iye, m'bwalo lina la m'tsogolo mwa khondelo, linamangidwa chimodzimodzi. Anammangiranso nyumba mwana wamkazi wa Farao, amene adamkwatira Solomoni, yofanafana ndi khonde limeneli. Izi zonse zinali za miyala ya mtengo wapatali yosemasema, malingana ndi miyeso yake, yocheka ndi mipeni ya manomano m'katimo ndi kunjako, kuyambira kumaziko kufikira kumutu, momwemonso kunjako ku bwalo lalikulu. Ndipo maziko ake anali a miyala ya mtengo wapatali, ndiyo miyala yaikulu, miyala ya mikono khumi, ndi miyala ya mikono isanu ndi itatu. Ndi pamwamba pake panali miyala ya mtengo wapatali, ndiyo miyala yosemasema monga muyeso wake, ndi mitengo yamkungudza. Ndipo bwalo lalikulu lozingapo linali ndi mizere itatu ya miyala yosemasema, ndi mzere umodzi wa mitanda yamkungudza, monga bwalo la pakati pa nyumba ya Yehova, ndi chipinda cholowera cha nyumbayo. Ndipo mfumu Solomoni anatuma anthu kukatenga Hiramu ku Tiro. Iyeyo anali mwana wake wa mkazi wamasiye wa fuko la Nafutali, atate wake anali munthu wa ku Tiro, mfundi wamkuwa; ndipo iye anadzala ndi nzeru ndi luntha ndi luso kugwira ntchito zonse za mkuwa. Ndipo anadza kwa mfumu Solomoni namgwirira ntchito zake zonse. Popeza iyeyu anaunda nsanamira ziwiri zamkuwa, msinkhu wake wa imodzi unali mikono khumi mphambu isanu ndi itatu; ndipo chingwe cha mikono khumi mphambu iwiri chinayesa thupi la nsanamira imodzi. Ndipo anapanga mitu iwiri ya mkuwa wosungunula, kuiika pamwamba pa nsanamirazo, msinkhu wake wa mutu wina unali mikono isanu, ndi msinkhu wa mutu unzake mikono isanu. Ndipo panali maukonde olukaluka ndi zoyangayanga, zokolana za pa mitu imene inali pamwamba pa nsanamira; zisanu ndi ziwiri za pa mutu wina, ndi zisanu ndi ziwiri za pa mutu unzake. M'mwemo anapanga nsanamira, ndipo panali mizere iwiri yozungulira ukonde umodzi, kukuta ndi makangaza mituyi inali pamwambapo, nachita momwemo ndi mutu winawo. Ndipo mituyi inali pamwamba pa nsanamira za pa chipinda cholowera chinali ngati akakombo malembedwe ake, a mikono inai. Ndipo panalinso mitu pamwamba pa nsanamira ziwirizo, pafupi pa mimbayo, inali m'mbali mwake mwa ukondewo; ndipo makangazawo anali mazana awiri, akukhala mizere yozinga ndanda mutu winawo. Ndipo anaimiritsa nsanamirazi pa chipinda cholowera cha Kachisi; naimiritsa nsanamira ya ku dzanja lamanja, natcha dzina lake Yakini; naimiritsa nsanamira yakumanzere, natcha dzina lake Bowazi. Ndipo pamwamba pa nsanamirazo panali ngati akakombo malembedwe ake; motero anaitsiriza ntchito ya nsanamirazo. Ndipo anayenganso thawale lamkuwa, kukamwa kwake kunali kwa mikono khumi, linali lozunguniza, ndi msinkhu wake unali mikono isanu; ndi chingwe cha mikono makumi atatu chinalizungulira. Ndipo m'khosi mwake munali ngati zikho zozinganiza m'mkono umodzi zikho khumi zakuzinganiza thawalelo; zikhozo zinayengedwa m'mizere iwiri poyengedwa thawalelo. Linasanjikika pa ng'ombe khumi mphambu ziwiri, zitatu zinapenya kumpoto, zitatu kumadzulo, zitatu kumwera, zitatu kum'mawa; ndipo thawalelo linakhazikika pamwamba pa izo; ndipo nkholo zao zinayang'anana. Ndipo kuchindikira kwake kunali ngati chikhato cha munthu, ndipo mlomo wake unasadamuka ngati mlomo wa chomwera, ngati maluwa akakombo, analowamo madzi a mitsuko yaikulu zikwi ziwiri. Ndipo anapanga maphaka khumi amkuwa, m'litali mwake mwa phaka limodzi mikono inai, ndi msinkhu wake mikono itatu. Ndipo mapangidwe a maphakawo anali otere: anali nao matsekerezo ao, ndipo matsekerezo anali pakati pa mbano. Ndipo pa matsekezerezo a pakati pa mbano panali ngati mikango ndi ng'ombe ndi akerubi, ndi pamwamba pa mbano panali chosanjikirapo; ndipo pansi pa mikango ndi ng'ombe panaphatikizika zotsetseremba zoyangayanga zokoloweka. Ndipo phaka lililonse linali ndi njinga zamkuwa zinai ndi mitanda yamkuwa, ndipo ngodya zake zinai zinali ndi mapewa; pansi pa thawale panali mapewa oyengeka pa mbali pa zophatikizika zonse. Ndipo pakamwa pake m'katimo pamwamba pa chosanjikira, panayesa mkono umodzi; koma pakamwa pake panali posadamuka, monga mapangidwe ake a chosanjikira, mkono umodzi ndi nusu; ndiponso pakamwa pake panali zolemba ndi matsekerezo ake anali aphwamphwa, si ozunguniza. Ndipo njinga zinai zinali pansi pa matsekerezo, ndi mitanda ya njinga inali m'mphakamo, ndi msinkhu wa njinga imodzi unali mkono umodzi ndi nusu. Ndipo mapangidwe a njinga analingana ndi mapangidwe a njinga za galeta, mitanda yake ndi mkombero wake ndi nthiti zake ndi mtima wake zonsezo zinayengedwa. Ndipo panali ngati mapewa anai pansi pangodya zinali za phaka limodzi, mapewawo anali a phaka lomwelo. Ndipo pamwamba pa phaka panali khoma lozunguniza, msinkhu wake nusu ya mkono; ndi pamwamba pa phaka panali mbano zake ndi matsekerezo a phaka lomwelo. Ndipo m'mapanthi mwa mbano zake ndi pa matsekerezo ake analemba ngati akerubi ndi mikango ndi migwalangwa, monga mwa malo ake a zonsezo, ndi zoyangayanga zozungulira. Motero anapanga maphaka khumiwo, anafanana mayengedwe ao muyeso wao ndi maonekedwe ao. Ndipo anapanga mbiya zaphwamphwa khumi zamkuwa; m'mbiya imodziyo munalowamo madzi a mitsuko yaikulu makumi anai, ndipo mbiya iliyonse inali ya mikono inai: pa phaka lililonse la maphaka aja khumi panakhala mbiya imodzi. Ndipo anaika maphaka asanu ku dzanja lamanja la nyumba, ndi maphaka asanu ku dzanja lamanzere la nyumba; naika thawalelo ku dzanja lamanja la nyumba kum'mawa kupenya kumwera. Ndipo Hiramu anayenga mbiyazo ndi zoolera ndi mbale zowazira. Motero Hiramu anatsiriza kupanga ntchito yonse anaichitira mfumu Solomoni ya m'nyumba ya Yehova. Nsanamira ziwirizo, ndi mbale za mitu inali pamwamba pa nsanamira ziwirizo, ndi maukonde awiri ophimbira mbale ziwiri za mitu inali pamwamba pa nsanamirazo, ndi makangaza mazana anai a maukonde awiriwo, mizere iwiri ya makangaza a ukonde umodzi kuphimbira mbale ziwiri za mitu inali pa nsanamirazo, ndi maphaka khumiwo ndi mbiya khumi zili pa maphakawo, ndi thawale limodzilo, ndi ng'ombe khumi mphambu ziwirizo pansi pa thawale; ndi miphikayo, ndi zoolerazo, ndi mbalezo; inde zotengera zonse zimene Hiramu anampangira mfumu Solomoni za m'nyumba ya Yehova, zinali za mkuwa wonyezimira. Mfumu inaziyenga pa chidikha cha ku Yordani, m'dothi ladongo, pakati pa Sukoti ndi Zaretani. Ndipo Solomoni anazileka zipangizo zonse osaziyesa, popeza zinachuluka ndithu; kulemera kwake kwa mkuwa wonsewo sikunayeseka. Ndipo Solomoni anapanga zipangizo zonse za m'nyumba ya Yehova: guwa la nsembe lagolide, ndi gome lagolide loikapo mikate yoonekera; ndi zoikapo nyali za golide woyengetsa, zisanu ku dzanja lamanja, zisanu kulamanzere, chakuno cha chipinda chamkati, ndi maluwa ndi nyali ndi mbano zagolide; ndi zikho, ndi zozimira nyali, ndi mbale, ndi zipande, ndi zopalira moto za golide woyengetsa, ndi zomangira zitseko zagolide, za zitseko za chipinda cha m'katimo, malo opatulika kwambiri, ndiponso za zitseko za nyumba ya Kachisi. Motero ntchito zonse zinatsirizika, zimene mfumu Solomoni anachitira nyumba ya Yehova. Ndipo Solomoni analonga zinthu adazipatula Davide atate wake, ndizo siliva ndi golide ndi zipangizo zomwe naziika mosungira chuma cha nyumba ya Yehova. Pamenepo Solomoni anasonkhanitsa akulu a Israele, ndi akulu onse a mafuko, akalonga a nyumba za atate a ana a Israele, kwa mfumu Solomoni m'Yerusalemu, kukatenga likasa la chipangano cha Yehova m'mudzi wa Davide, ndiwo Ziyoni. Ndipo anthu onse a Israele anasonkhana kwa mfumu Solomoni kukadyerera m'mwezi wa Etanimu, ndiwo mwezi wachisanu ndi chiwiri. Ndipo akulu onse a Israele anadza, ansembe nanyamula likasa. Ndipo anatenga likasa la Yehova, ndi chihema chokomanako, ndi zipangizo zonse zopatulika, zinali m'chihemamo, inde zimenezi anazitenga ansembe ndi Alevi. Ndipo mfumu Solomoni ndi msonkhano wonse wa Israele wosonkhana kwa iye anali naye kulikasa, naphera nkhosa ndi ng'ombe za nsembe zosawerengeka ndi zosadziwika, chifukwa cha unyinji wao. Ndipo ansembe analonga likasa la chipangano cha Yehova kumalo kwake, ku chipinda chamkati, ku malo opatulika kwambiri, munsi mwa mapiko a akerubi. Popeza akerubiwo anatambasula mapiko ao awiri pamwamba pa likasa, ndipo akerubiwo anaphimba pamwamba pa likasa ndi mphiko zake. Ndipo mphikozo zinatalika kuti nsonga za mphiko zidaoneka ku malo opatulika chakuno cha chipinda chamkati; koma sizinaoneka kubwalo; ndipo zikhala pomwepo mpaka lero lino. Munalibe kanthu m'likasamo koma magome awiri aja a mwala Mose anawalongamo pa Horebu, pamene Yehova anapangana ndi ana a Israele, potuluka iwo m'dziko la Ejipito. Ndipo kunachitika atatuluka ansembe m'malo opatulika, mtambo unadzaza nyumba ya Yehova. Ndipo ansembe sanakhoze kuimirira kutumikira chifukwa cha mtambowo, popeza ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehova. Pamenepo Solomoni anati, Yehova ananena kuti adzakhala m'mdima waukulu. Ine ndakumangirani ndithu nyumba yokhalamo Inu, ndiyo malo okhalamo Inu nthawi zosatha. Ndipo mfumu inapotoloka nkhope yake, nidalitsa msonkhano wonse wa Israele. Ndi msonkhano wonse wa Israele unaimirira. Nati iye, Wolemekezeka ndi Yehova Mulungu wa Israele amene analankhula m'kamwa mwake ndi Davide atate wanga, nakwaniritsa ndi dzanja lake, nati, Kuyambira tsiku lakutulutsa Ine anthu anga Aisraele m'dziko la Ejipito, sindinasankha mudzi uliwonse mwa mafuko onse a Israele kumangamo nyumba yokhalamo dzina langa, koma ndinasankha Davide kukhala mfumu ya anthu anga Aisraele. Ndipo Davide atate wanga anafuna m'mtima mwake kumangira dzina la Yehova Mulungu wa Israele nyumba. Koma Yehova ananena ndi Davide atate wanga, Popeza unafuna m'mtima mwako kumangira dzina langa nyumba, unachita bwino kuti m'mtima mwako unatero. Koma usamange ndiwe nyumbayo, koma mwana wako adzatuluka m'chuuno mwako, iyeyo adzamangira dzina langa nyumba. Ndipo Yehova wakhazikitsa mau ake analankhulawo, ndipo ndauka ndine m'malo mwa Davide atate wanga, ndipo ndikhala pa mpando wachifumu wa Israele monga adalonjeza Yehova, ndipo ndamangira dzina la Yehova Mulungu wa Israele nyumba. Ndipo ndakonzera malo likasalo, m'mene muli chipangano cha Yehova, chimene anapangana ndi makolo athu pamene anawatulutsa m'dziko la Ejipito. Ndipo Solomoni anaimirira ku guwa la nsembe la Yehova pamaso pa msonkhano wonse wa Israele, natambasulira manja ake kumwamba, nati, Yehova Mulungu wa Israele, palibe Mulungu wolingana ndi Inu m'thambo la kumwamba, kapena pa dziko lapansi, wakusungira chipangano ndi chifundo akapolo anu akuyenda ndi mtima wonse pamaso panu, wakusungira mtumiki wanu Davide atate wanga chimene mudamlonjezacho; munalankhulanso m'kamwa mwanu ndi kukwaniritsa ndi dzanja lanu monga lero lino. Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israele, msungireni mtumiki wanu Davide atate wanga chimene chija mudamlonjezacho, ndi kuti, Sadzakusowa munthu pamaso panga wokhala pa mpando wachifumu wa Israele; komatu ana ako achenjere njira yao, kuti akayende pamaso panga monga umo unayendera iwe pamaso panga. Ndipo tsopano, Mulungu wa Israele, atsimikizike mau anu amene munalankhula ndi mtumiki wanu Davide atate wanga. Kodi Mulungu adzakhala ndithu pa dziko lapansi? Taonani, thambo ndi m'Mwambamwamba zichepa kukulandirani, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimangayi. Koma mucheukire pemphero la kapolo wanu, ndi pembedzero lake, Yehova Mulungu wanga, kumvera kulira ndi kupempha kwake kumene kapolo wanu apempha pamaso panu lero; kuti maso anu atsegukire nyumba yino usiku ndi usana, kumalo kumene munanenako, Dzina langa lidzakhala komweko; kuti mumvere pemphero limene adzapemphera kapolo wanu lolunjika kumalo kuno. Ndipo mverani pembedzero la kapolo wanu ndi la anthu anu Aisraele, pamene adzapemphera molunjika kumalo kuno; ndipo mverani Inu m'Mwamba mokhala Inumo; ndipo pamene mukumva, khululukirani. Ngati munthu akachimwira mnzake, ndi lumbiro likaikidwa pa iye kumlumbiritsa, ndipo akadzalumbira patsogolo pa guwa la nsembe lanu m'nyumba yino; mverani Inu pamenepo m'mwambamo, ndipo chitani, weruzani akapolo anu, kumtsutsa woipayo, ndi kumbwezera tchimo lake, ndi kulungamitsa wolungamayo kumbwezera monga chilungamo chake. Ndipo anthu anu Aisraele akawakantha adani ao chifukwa cha kuchimwira Inu, ndipo akabweranso kwa Inu, ndi kuvomereza dzina lanu, ndi kupemphera, ndi kupembedza Inu m'nyumba muno; pamenepo mverani Inu m'Mwambamo, ndi kukhululukira tchimo la anthu anu Aisraele, ndi kuwabwezera ku dziko limene munapatsa makolo ao. Pamene kumwamba kwatsekera, ndipo kulibe mvula chifukwa cha kuchimwira Inu, nakapemphera iwo molunjika kumalo kuno, ndi kuvomereza dzina lanu, ndi kutembenuka kusiya zoipa zao, pakuwasautsa Inu; pamenepo mverani Inu m'Mwamba, ndi kukhululukira tchimo la akapolo anu, ndi la anthu anu Aisraele; pakuti muwaphunzitsa njira yokoma ayenera kuyendamo, ndi kupatsa mvula pa dziko lanu, limene munawapatsa anthu anu likhale cholowa chao. M'dziko mukakhala njala, mukakhala mliri, mlaza, chinoni, dzombe, kapena kapuchi, adani ao akawamangira misasa m'dziko la midzi yao, mukakhala mliri uliwonse, kapena nthenda; tsono pempho ndi pembedzero lililonse akalipempha munthu aliyense, kapena anthu anu onse Aisraele, pakuzindikira munthu yense chinthenda cha mtima wa iye yekha, ndi kutambasulira manja ake kunyumba yino; pamenepo mverani Inu m'Mwamba mokhala Inu, ndi kukhululukira, ndi kuchita, ndi kubwezera munthu yense monga njira zake zonse, amene Inu mumdziwa mtima wake, popeza Inu, Inu nokha, mudziwa mitima ya ana onse a anthu; kuti aope Inu masiku onse akukhala iwowo m'dziko limene Inu munapatsa makolo ao. Ndiponso kunena za mlendo, wosati wa anthu anu Aisraele, koma wakufumira m'dziko lakutali chifukwa cha dzina lanu, popeza adzamva za dzina lanu lalikulu ndi dzanja lanu lamphamvu ndi mkono wanu wotambasuka; akabwera iyeyo nadzapemphera molunjika kunyumba yino; mverani Inu m'Mwamba mokhala Inu, ndipo chitani monga mwa zonse mlendoyo azipempha kwa Inu; kuti anthu onse a dziko lapansi adziwe dzina lanu, kuopa Inu, monga amatero anthu anu Aisraele, ndi kuti adziwe kuti nyumba yino ndaimangayi yatchedwa dzina lanu. Akatuluka anthu anu kukayambana nkhondo ndi adani ao, kumene konse Inu mudzawatuma, ndipo akapemphera kwa Yehova molunjika kumudzi uno munausankha Inu, ndi kunyumba ndamangira dzina lanu; pamenepo mverani Inu m'Mwamba pempho ndi pembedzero lao, ndi kulimbitsa mlandu wao. Akachimwira Inu, popeza palibe munthu wosachimwa, ndipo mukakwiya nao ndi kuwapereka kwa adani, kuti iwo awatenge ndende kunka nao ku dziko la adani, ngati kutali kapena kufupi, ndipo akakumbukira mitima yao, ali kudziko kumene anatengedwa ukapolo, nakalapa, nakapembedza Inu m'dziko iwo anawatenga ndende, ndi kuti, Tachimwa, ndipo tachita mphulupulu, tachita moipa; ndipo akabwerera kwa Inu ndi mtima wao wonse ndi moyo wao wonse, m'dziko la adani ao adawatenga ndendewo, ndipo akapemphera kwa Inu molunjika ku dziko lao munapatsa makolo aolo, kumudzi munausankha Inu, ndi kunyumba ndamangira dzina lanu; pamenepo mverani Inu pemphero ndi pembedzero lao m'Mwamba mokhala Inumo, ndi kulimbitsa mlandu wao, ndi kukhululukira anthu anu adachimwira Inu ndi mphulupulu zao zonse adapalamula nazo kwa Inu; ndipo muwachititsire chifundo iwo amene anawagwira ndende, kuti awachitire chifundo; pakuti awa ndi anthu anu ndithu, ndi cholowa chanu chimene munatulutsa m'Ejipito, m'kati mwa ng'anjo ya chitsulo; kuti maso anu akatsegukire pembedzero la kapolo wanu ndi pembedzero la anthu anu Aisraele, kuwamvera m'mene monse akafuula kwa Inu. Popeza Inu munawapatula pa anthu onse a pa dziko lapansi akhale cholowa chanu, monga munanena ndi dzanja la Mose mtumiki wanu, pamene munatulutsa makolo athu m'Ejipito, Yehova Mulungu Inu. Ndipo kunali kuti atatsiriza Solomoni kupemphera kwa Yehova pemphero ndi pembedzero lino lonse, ananyamuka ku guwa la nsembe la Yehova pomwe analikugwada pa mabondo ake, ndi manja ake otambasulira kumwamba. Naimirira, nadalitsa msonkhano wonse wa Israele ndi mau okweza, nati, Wolemekezeka ndi Yehova amene anapumulitsa anthu ake Aisraele, monga mwa zonse analonjezazo; sanatayike mau amodzi a mau ake onse abwino, amene analankhula ndi dzanja la Mose mtumiki wake. Yehova Mulungu wathu akhale nafe monga umo anakhalira nao makolo athu, asatisiye kapena kutitaya; kuti atitembenuzire kwa Iye yekha mitima yathu iyende m'njira zake zonse, ndi kusunga malamulo ake onse ndi malemba ake ndi maweruzo ake, amene anawalamulira makolo athu. Ndipo mau anga amenewa ndapembedzera nao pamaso pa Yehova akhale pafupi ndi Yehova Mulungu wathu usana ndi usiku, kuti alimbitse mlandu wa kapolo wake, ndi mlandu wa anthu ake Aisraele, mlandu wa tsiku pa tsiku lake; kuti anthu onse a pa dziko lapansi akadziwe kuti Yehova ndiye Mulungu, palibe wina. Mitima yanu ikhale yangwiro ndi Yehova Mulungu wathu, kuyenda m'malemba ake ndi kusunga malamulo ake, monga lero lino. Ndipo mfumu ndi anthu onse a Israele pamodzi naye anaphera nsembe pamaso pa Yehova. Ndipo Solomoni anaphera nsembe yamtendere, yophera kwa Yehova ng'ombe zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, ndi nkhosa zikwi zana limodzi mphambu makumi awiri. Momwemo mfumu ndi ana a Israele onse anapereka nyumbayo ya Yehova. Tsiku lomwelo mfumu inapatulira Mulungu pakati pake pa bwalo la ku khomo la nyumba ya Yehova; pakuti pomwepo anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe yaufa, ndi mafuta a nsembe zamtendere; popeza guwa la nsembe lamkuwa linali pamaso pa Yehova lidachepa kulandira nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi mafuta a nsembe zamtendere. Ndipo nthawi yomweyo Solomoni anachita madyerero pamaso pa Yehova Mulungu wathu, ndi Israele yense pamodzi naye, msonkhano waukulu wakuyambira polowera ku Hamati kufikira ku nyanja ya ku Ejipito, masiku asanu ndi awiri, ndi masiku asanu ndi awiri ena, ndiwo masiku khumi mphambu anai. Tsiku lachisanu ndi chitatu anawauza anthu apite; ndipo iwo anadalitsa mfumu, napita ku mahema ao osekera ndi okondwera mtima chifukwa cha zokoma zonse Yehova anachitira Davide mtumiki wake, ndi Israele anthu ake. Ndipo kunali, atasiriza Solomoni kumanga nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi chifuniro chonse cha Solomoni anachikhumbacho, Yehova anaonekera kwa Solomoni nthawi yachiwiri, monga momwe adamuonekera ku Gibiyoni. Ndipo Yehova anati kwa iye, Ndamva pemphero lako ndi pembedzero lako wandipembedza nalo; ndapatula nyumba imene waimangayi kuikamo dzina langa nthawi zosatha, ndipo maso anga ndi mtima wanga zidzakhala kumeneko masiku onse. Ndipo iwe ukadzayenda pamaso panga, monga momwe Davide atate wako anayendera ndi mtima woona ndi wolungama, kuzichita zonse ndakulamulirazo, ndi kusunga malemba anga ndi maweruzo anga, pamenepo Ine ndidzakhazikitsa chimpando cha ufumu wako pa Israele nthawi yosatha, monga ndinalonjezana ndi Davide atate wako, ndi kuti, Sadzakusowa munthu wamwamuna pa mpando wachifumu wa Israele. Koma mukadzabwerera pang'ono pokha osanditsata, kapena inu, kapena ana anu, osasunga malamulo anga ndi malemba anga amene ndawaika pamaso panu; mukadzatumikira milungu ina ndi kuilambira; pamenepo Ine ndidzalikha Aisraele kuwachotsera m'dziko ndidawapatsali; ndipo nyumba yino ndapatulira dzina langayi ndidzaitaya kosapenyeka; ndipo Israele adzakhala ngati mwambi ndi nkhani pakati pa anthu onse. Ndipo munthu yense wopitirira pa nyumba yaitali yino adzadabwa nayo, nadzainyoza, nadzati, Yehova watero chifukwa ninji ndi dziko lino ndi nyumba yino? Ndipo anthu adzayankha, Popeza anasiya Yehova Mulungu wao amene adatulutsa makolo ao m'dziko la Ejipito, natsata milungu ina, nailambira, naitumikira; chifukwa chake Yehova anawagwetsera choipa chonsechi. Ndipo kunali, zitatha zaka makumi awiri m'mene Solomoni adatsiriza nyumba ziwirizo, ndizo nyumba ya Yehova ndi nyumba ya mfumu; popeza Hiramu mfumu ya Tiro adamthandiza Solomoni ndi mitengo yamkungudza ndi yamlombwa ndi golide yemwe, monga momwe iye anafuniramo, chifukwa chake mfumu Solomoni anampatsa Hiramu midzi makumi awiri m'dziko la Galileya. Ndipo Hiramu anatuluka ku Tiro kukaona midzi adampatsa Solomoniyo, koma siinamkomera. Nati, Midzi yino mwandipatsayi njotani, mbale wanga? Naitcha dzina lao, Dziko lachikole, kufikira lero lino. Ndipo Hiramu adatumiza kwa mfumu matalente a golide zana limodzi mphambu makumi awiri. Ndipo chifukwa chake cha msonkho uja anausonkhetsa mfumu Solomoni ndi chimenechi; kuti amange nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya iye yekha, ndi Milo, ndi linga la Yerusalemu, ndi Hazori, ndi Megido, ndi Gezere. Pakuti Farao mfumu ya Aejipito adakwera nalanda Gezere, nautentha ndi moto, nawapha Akanani akukhala m'mudzimo, naupereka kwaulere kwa mwana wake mkazi wa Solomoni. Ndipo Solomoni anamanganso Gezere, ndi Betehoroni wakunsi, ndi Baalati, ndi Tamara wa m'chipululu m'dziko muja, ndi midzi yonse yosungamo zinthu zake za Solomoni, ndi midzi yosungamo magaleta ake, ndi midzi yokhalamo apakavalo ake, ndi zina zilizonse zidakomera Solomoni kuzimanga m'Yerusalemu, ndi ku Lebanoni, ndi m'dziko lonse la ufumu wake. Ndipo Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi otsala, amene sanali a ana a Israele, ana ao amene adatsala m'dziko, amene ana a Israele sanakhoze kuononga konse, Solomoni anawasenzetsa msonkho wa ntchito kufikira lero. Koma Solomoni sanawayese ana a Israele akapolo, koma iwowo anali anthu a nkhondo, ndi anyamata ake, ndi akalonga ake, ndi akazembe ake, ndi oyang'anira magaleta ake ndi apakavalo ake. Ameneyo anali akulu a kapitao oyang'anira ntchito ya Solomoni, mazana asanu mphambu makumi asanu akulamulira anthu ogwira ntchito aja. Koma mwana wamkazi wa Farao anatuluka m'mudzi wa Davide kukwera kunyumba yake adammangira Solomoni, pamenepo iye anamanganso Milo. Ndipo chaka chimodzi Solomoni anapereka katatu nsembe zopsereza ndi zamtendere, pa guwa la nsembe limene anammangira Yehova, nafukiza zonunkhira pa guwa la nsembe pamaso pa Yehova, atatsiriza nyumbayo. Ndipo mfumu Solomoni anamanga zombo zambiri ku Eziyoni-Gebere uli pafupi ndi Eloti, m'mphepete mwa Nyanja Yofiira, ku dziko la Edomu. Ndipo, Hiramu anatuma anyamata ake m'zombozo amalinyero ozolowera m'nyanja, pamodzi ndi anyamata a Solomoni. Ndipo iwo anafika ku Ofiri, natengako golide matalente mazana anai mphambu makumi awiri, nafika naye kwa mfumu Solomoni. Ndipo atamva mfumu yaikazi ya ku Sheba mbiri ya Solomoni yakubukitsa dzina la Yehova, anadza kumuyesera iye ndi miyambi yododometsa. Nafika ku Yerusalemu ndi ulendo wake waukulu, ndi ngamira zakunyamula zonunkhira, ndi golide wambiri, ndi timiyala ta mtengo wapatali; ndipo atafika kwa Solomoni anakamba naye zonse za m'mtima mwake. Ndipo Solomoni anamyankha miyambi yake yonse, panalibe kanthu kobisika ndi mfumu kamene sanamfotozere iye. Ndipo pamene mfumu yaikazi ya ku Sheba adaona nzeru zonse za Solomoni, ndi nyumba adaimangayo, ndi zakudya za pa gome lake, ndi makhalidwe a anyamata ake, ndi maimiriridwe a atumiki ake, ndi zovala zao, ndi otenga zikho ake, ndi nsembe yake yopsereza imene amapereka m'nyumba ya Yehova, anakhululuka malungo. Ndipo anati kwa mfumu, Idali yoonadi mbiri ija ndinaimva ine ku dziko langa ya machitidwe anu ndi nzeru zanu. Koma sindinakhulupirira mau amenewo mpaka ndafika ine kuno, ndaona ndi maso anga; ndipo taonani, anangondiuza dera lina lokha; nzeru zanu ndi zokoma zanu zakula pa mbiri ndinaimvayo. Odala anthu anu, odala anyamata anu akukhala nthawi zonse pamaso panu, akumvaimva nzeru yanu. Wolemekezeka Yehova Mulungu wanu amene anakondwera nanu, kukuikani pa mpando wachifumu wa Israele; popeza Yehova anakonda Israele nthawi yosatha, chifukwa chake anakulongani inu ufumu, kuti muchite chiweruzo ndi chilungamo. Ndipo mkaziyo ananinkha mfumu matalente a golide zana limodzi mphambu makumi awiri, ndi zonunkhira zaunyinji ndi timiyala ta mtengo wapatali; sunafikanso unyinji wotero wa zonunkhira wolingana ndi uja mfumu yaikazi ya ku Sheba inapereka kwa mfumu Solomoni. Ndipo zombo za Hiramu zotengera golide ku Ofiri zinatenganso ku Ofiri mitengo yambiri yambawa, ndi timiyala ta mtengo wapatali. Ndipo mfumu inasema mitengo yambawayo, ikhale mizati ya nyumba ya Yehova, ndi ya nyumba ya mfumu; ndiponso azeze ndi zisakasa za oimbawo; siinafika kapena kuonekanso mpaka lero mitengo yotero yambawa. Ndipo mfumu Solomoni ananinkha mfumu yaikazi ya ku Sheba chifuniro chake chonse anachipempha iye, osawerenga chimene Solomoni anamninkha mwa ufulu wake. Momwemo iye anabwerera namukanso ku dziko lake, iyeyo ndi anyamata ake. Tsono kulemera kwake kwa golide anafika kwa Solomoni chaka chimodzi kunali matalente mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi limodzi a golide. Osawerenganso winayo wa anthu a malonda oyendayenda, ndi wa amalonda ena, ndi wa mafumu onse a Arabiya, ndi wa akazembe onse a madera. Ndipo mfumu Solomoni anapanga zikopa mazana awiri zagolide wonsansantha, chikopa chimodzi chinapangidwa ndi masekeli mazana asanu ndi limodzi. Ndi malihawo mazana atatu a golide wonsansantha, lihawo limodzi linapangidwa ndi miyeso ya mina itatu ya golide; ndipo mfumu inazisungira zonse m'nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni. Ndipo mfumu inapanga mpando waukulu wachifumu waminyanga, naukuta ndi golide woyengetsa. Mpandowo wachifumu unali ndi makwerero asanu ndi limodzi, ndi pamwamba pa mpando wachifumu panali pozunguniza kumbuyoko, ndipo munali ngati manja m'mbali zonse ziwiri za pokhalirapo, naimika mikango iwiri m'mbali mwa manjawo. Ndipo anaimika mikango khumi ndi iwiri mbali ina ndi ina, pa makwerero asanu ndi limodzi aja; m'dziko lililonse lina simunapangidwa wotere. Ndipo zikho zomwera zonse za mfumu Solomoni zinali zagolide, ndi zotengera zonse za nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni zinali zagolide yekhayekha, panalibe zasiliva, pakuti siliva anangoyesedwa opanda pake masiku onse a Solomoni. Popeza mfumu inali nazo panyanja zombo za ku Tarisisi, pamodzi ndi zombo za Hiramu; zombo za ku Tarisisi zinafika kamodzi zitapita zaka zitatu, zili nazo golide, ndi siliva, ndi minyanga, ndi apusi, ndi mbalame za zitsukwa zazitali za mawangamawanga. Ndipo mfumu Solomoni anawaposa mafumu onse a dziko lapansi pa chuma ndi nzeru. Ndipo anthu onse a pa dziko anafuna nkhope ya Solomoni, kudzamva nzeru zake zimene Mulungu analonga m'mtima mwake. Ndipo akafika munthu yense ndi mtulo wake, zotengera zasiliva, ndi zotengera zagolide, ndi zovala, ndi mure, ndi zonunkhira, ndi akavalo, ndi nyuru; momwemo chaka ndi chaka. Ndipo Solomoni anasonkhanitsa magaleta ndi apakavalo; anali nao magaleta chikwi chimodzi mphambu mazana anai, ndi apakavalo zikwi khumi mphambu ziwiri, nawasungira m'midzi yosungamo magaleta, ndi kwa mfumu m'Yerusalemu. Ndipo mfumu inachulukitsa siliva ngati miyala m'Yerusalemu, ndi mitengo yamikungudza anailinganiza ndi mikuyu ya m'madambo. Ndipo akavalo a Solomoni anachokera ku Ejipito; anthu a malonda a mfumu anawagula magulumagulu, gulu lililonse mtengo wake. Ndipo galeta limodzi linachokera kutuluka m'Ejipito mtengo wake masekeli a siliva mazana asanu ndi limodzi, ndi kavalo mtengo wake masekeli zana limodzi mphambu makumi asanu; momwemonso iwo anawagulira mafumu onse a Ahiti ndi mafumu a Aramu. Ndipo mfumu Solomoni anakonda akazi ambiri achilendo, pamodzi ndi mwana wamkazi wa Farao, akazi a ku Mowabu, ndi a ku Amoni, ndi a ku Edomu, ndi a ku Sidoni, ndi Ahiti; a mitundu ija Yehova adanena ndi ana a Israele za iwo, kuti, Inu musakalowa kwa iwo, ndipo iwo asadzalowe kwa inu; zedi adzatembenuza mitima yanu kutsata milungu yao; amenewo Solomoni anawaumirira kuwakonda. Ndipo anali nao akazi mazana asanu ndi awiri, ana akazi a mafumu, ndi akazi aang'ono mazana atatu; ndipo akazi ake anapambutsa mtima wake. Ndipo kunali, atakalamba Solomoni, akazi ake anapambutsa mtima wake atsate milungu ina; ndipo mtima wake sunakhala wangwiro ndi Yehova Mulungu wake monga mtima wa Davide atate wake. Tsono Solomoni anatsata Asitoreti fano la anthu a Sidoni, ndi Milikomu fano lonyansitsa la Aamoni. Ndipo Solomoni anachita choipa pamaso pa Yehova, osatsata Yehova ndi mtima wonse monga Davide atate wake. Pamenepo Solomoni anamangira Kemosi fano lonyansitsa la Amowabu ndi Moleki fano lonyansitsa la ana a Amoni misanje, pa phiri lili patsogolo pa Yerusalemu. Ndipo momwemo anachitiranso akazi ake onse achilendo, amene amafukizira naphera nsembe mafano ao. Ndipo Yehova anakwiya ndi Solomoni, pokhala mtima wake unapatuka kwa Yehova Mulungu wa Israele, amene adamuonekera kawiri, namlamulira za chinthu chomwechi, kuti asatsate milungu ina, koma iye sanasunge chimene Yehova anachilamula. Chifukwa chake Yehova ananena ndi Solomoni, Popeza chinthu ichi chachitika ndi iwe, ndipo sunasunga chipangano changa ndi malemba anga amene ndinakulamulira, zedi, ndidzakung'ambira ufumu ndi kuupatsa mnyamata wako. Koma m'masiku ako sindidzatero chifukwa cha Davide atate wako, koma ndidzaung'ambira m'manja mwa mwana wako; komatu sindidzachotsa ufumu wonsewo; fuko limodzi ndidzapatsa mwana wako, chifukwa cha Davide mtumiki wanga, ndi chifukwa cha Yerusalemu amene ndinamsankha. Ndipo Yehova anamuutsira Solomoni mdani, ndiye Hadadi Mwedomu; iyeyo anali wa mbumba ya mfumu ya ku Edomu. Pakuti pamene Davide adali m'Edomu, ndipo Yowabu kazembe wa nkhondo adanka kukaika akufawo, atapha amuna onse m'Edomu; pakuti Yowabu ndi Aisraele onse anakhalako miyezi isanu ndi umodzi, mpaka atawapha amuna onse m'Edomu; Hadadi uja anathawa, iyeyo ndi a ku Edomu ena, akapolo a atate wake pamodzi naye, kunka ku Ejipito, Hadadiyo akali mwana. Ndipo anachoka ku Midiyani nafika ku Parani, natenga anthu a ku Parani pamodzi nao, nafika ku Ejipito kwa Farao mfumu ya Aejipito, ameneyo anampatsa nyumba, namnenera zakudya, nampatsako dziko. Ndipo Farao anamkomera mtima ndithu Hadadiyo, nampatsa mkazi ndiye mbale wa mkazi wake, mbale wake wa Tapenesi mkazi wamkulu wa mfumu. Ndipo mbale wa Tapenesi anamuonera Genubati mwana wake, ameneyo Tapenesi anamletsera kuyamwa m'nyumba ya Farao, ndipo Genubati anakhala m'banja la Farao pamodzi ndi ana amuna a Farao. Ndipo atamva Hadadi ku Ejipito kuti Davide anagona ndi makolo ake, ndi kuti Yowabu kazembe wa nkhondo adafanso, Hadadi ananena ndi Farao, Mundilole ndimuke ku dziko la kwathu. Tsono Farao anati kwa iye, Koma chikusowa iwe nchiyani kwa ine, kuti ufuna kumuka ku dziko la kwanu? Nayankha iye, Palibe kanthu, koma mundilole ndimuke ndithu. Ndipo Mulungu anamuutsira mdani wina, ndiye Rezoni mwana wa Eliyada, amene adathawa mbuye wake Hadadezere mfumu ya ku Zoba. Iye nasonkhanitsa anthu, nakhala kazembe wa nkhondo, muja Davide anawapha a ku Zobawo, napita ku Damasiko, nakhala komweko, nakhala mfumu ya ku Damasiko. Ndipo iye anali mdani wa Israele masiku onse a Solomoni, kuonjezerapo choipa anachichita Hadadi, naipidwa nao Aisraele, nakhala mfumu ya ku Aramu. Ndipo Yerobowamu mwana wa Nebati Mwefuremu wa ku Zereda mnyamata wa Solomoni, dzina la amake ndiye Zeruya, mkazi wamasiye, iyenso anakweza dzanja lake pa mfumu. Ndipo chifukwa chakukweza iye dzanja lake pa mfumu ndi chimenechi: Solomoni anamanga Milo, namanganso pogumuka pa linga la mudzi wa Davide atate wake. Ndipo munthu ameneyo Yerobowamu anali ngwazi; ndipo pamene Solomoni anamuona mnyamatayo kuti ngwachangu, anamuika akhale woyang'anira wa ntchito yonse ya nyumba ya Yosefe. Ndipo kunali nthawi yomweyo kuti Yerobowamu anatuluka m'Yerusalemu, ndipo mneneri Ahiya wa ku Silo anampeza m'njira; tsono iyeyo anavaliratu chovala chatsopano, ndipo iwo awiri anali okha kuthengo, Ndipo Ahiyayo anagwira chovala chake chatsopano, naching'amba khumi ndi pawiri. Nati kwa Yerobowamu, Takwaya magawo khumi; popeza atero Yehova Mulungu wa Israele, Taona ndidzaung'amba ufumu m'dzanja la Solomoni ndi kukupatsa iwe mafuko khumi. Koma iye adzakhala nalo fuko limodzi, chifukwa cha Davide mtumiki wanga, ndi cha Yerusalemu, mudzi umene ndinausankha m'mafuko onse a Israele. Nditero popeza iwo anandisiya, napembedza Asitoreti mulungu wa Asidoni, ndi Kemosi mulungu wa Amowabu, ndi Milikomu mulungu wa ana a Amoni, osayenda m'njira zanga, kuchita chimene chiyenera pamaso panga, ndi kusunga malemba anga ndi maweruzo anga, monga umo anatero Davide atate wake. Koma sindidzalanda ufumu wonse m'dzanja lake, koma ndidzamkhalitsa mfumu masiku ake onse, chifukwa cha Davide mtumiki wanga amene uja ndinamsankha, chifukwa kuti anasunga malamulo anga ndi malemba anga. Koma ndidzalanda ufumu m'dzanja la mwana wake, ndi kupatsa iwe mafuko khumi amene. Ndipo ndidzamninkha mwana wake fuko limodzi, kuti Davide mtumiki wanga akhale chikhalire ndi nyali pamaso panga m'Yerusalemu, mudzi umene ndinadzisankhira kuikapo dzina langa. Ndipo ndidzakutenga iwe, ndipo udzachita ufumu monga umo ukhumbira moyo wako, nudzakhala mfumu ya Israele. Ndipo kudzakhala kuti ukadzamvera iwe zonse ndikulamulirazo, nukadzayenda m'njira zanga ndi kuchita chilungamo pamaso panga, kusunga malemba anga ndi malamulo anga, monga anatero Davide mtumiki wanga pamenepo Ine ndidzakhala ndi iwe, ndidzakumangira ndi kukukhazikitsira nyumba, monga ndinammangira Davide, ndipo ndidzakupatsa iwe Israele. Ndipo chifukwa cha ichi ndidzazunza mbumba ya Davide, koma si masiku onse ai. Chifukwa chake Solomoni anafuna kupha Yerobowamu, ndipo Yerobowamu anathawira ku Ejipito kwa Sisake mfumu ya Aejipito, nakhala m'Ejipito kufikira imfa ya Solomoni. Ndipo machitidwe otsiriza a Solomoni, ndi ntchito zake zonse anazichita, ndi nzeru zake, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a Solomoni? Ndipo masiku amene Solomoni anakhala mfumu ya Aisraele onse m'Yerusalemu anali zaka makumi anai. Ndipo Solomoni anagona ndi makolo ake, naikidwa m'mudzi wa Davide atate wake; ndipo Rehobowamu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake. Ndipo Rehobowamu ananka ku Sekemu, popeza Aisraele onse anadza ku Sekemu kumlonga ufumu. Ndipo kunali kuti Yerobowamu mwana wa Nebati anachimva akali m'Ejipito, kumene anathawira kuchokera ku maso a Solomoni mfumu, pakuti Yerobowamu anakhala ku Ejipito. Ndipo anatuma kukamuitana. Ndipo Yerobowamu ndi msonkhano wonse wa Israele anadza, nalankhulana ndi Rehobowamu, nati, Atate wanu analemeretsa goli lathu, ndipo inu tsono pepuzaniko ntchito zosautsa za atate wanu, ndi goli lolemera lake limene anatisenza, ndipo tidzakutumikirani. Ndipo iye anati kwa iwo, Bamukani, mukagone masiku atatu, pamenepo mukabwera kwa ine. Ndipo anthu anamuka. Ndipo mfumu Rehobowamu anafunsira kwa mandoda, amene anaimirira pamaso pa Solomoni atate wake, akali moyo iyeyo, nati, Inu mundipangire bwanji kuti ndiyankhe anthu awa? Ndipo iwo anamuuza kuti, Mukakhala inu mtumiki wa anthu awa lero, ndi kuwatumikira ndi kuwayankha ndi kukamba nao mau okoma, tsono iwo adzakhala chikhalire atumiki anu. Koma iye analeka uphungu wa mandodawo, umene anampangirawo, nakafunsira kwa achinyamata anzake oimirira pamaso pake, nati kwa iwo, Kodi inu mundipangire bwanji kuti tiyankhe anthu awa anandiuza ine, kuti, Mupepuze goli limene atate wanu anatisenza ife? Ndipo achinyamata anzake ananena naye, nati, Mzitero ndi anthu awa adalankhula nanu, nati, atate wanu analemeretsa goli lathu, koma inu mutipepuzire limenelo; mzitero nao, Kanense wanga adzaposa m'chuuno mwa atate wanga. Ndipo tsopano, popeza atate wanga anakusenzani goli lolemera, ine ndidzaonjezerapo pa goli lanu, atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira. Ndipo Yerobowamu ndi anthu onse anabwera kwa Rehobowamu tsiku lachitatu monga momwe anawauzira mfumu, nati, Bweraninso kwa ine tsiku lachitatu. Ndipo mfumu inayankha anthu mau okalipa, naleka uphungu anampangira mandodawo, nalankhula nao monga mwa uphungu wa achinyamata, nati, Atate wanga analemeretsa goli lanu, koma ine ndidzaonjezerapo pa goli lanu; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakupulani ndi zinkhanira. Potero mfumu siinamvera anthuwo, pakuti kusintha uku kunachokera kwa Yehova, kuti akhazikitse mau ake amene Yehova ananenetsa Ahiya wa ku Silo kwa Yerobowamu mwana wa Nebati. Ndipo pakuona Aisraele onse kuti mfumu siinawamvera iwo, anthuwo anayankha mfumu, Tili naye chiyani Davide? Inde tilibe cholowa m'mwana wa Yese; tiyeni kwathu Aisraele inu; yang'aniranitu nyumba yako, Davide. Momwemo Aisraele anachoka kunka ku mahema ao. Koma ana aja a Israele akukhala m'midzi ya Yuda, Rehobowamu anakhalabe mfumu yao. Pamenepo mfumu Rehobowamu anatuma Adoramu wamsonkho, ndipo Aisraele onse anamponya miyala, nafa. Ndipo mfumu Rehobowamu anafulumira kulowa m'galeta wake kuthawira ku Yerusalemu. Motero Aisraele anapandukana ndi nyumba ya Davide kufikira lero. Ndipo kunali, atamva Aisraele onse kuti Yerobowamu wabweranso, anatuma kumuitanira iye kumsonkhano, namlonga iye mfumu ya Aisraele onse; palibe munthu anatsata nyumba ya Davide koma fuko lokha la Yuda. Ndipo Rehobowamu anafika ku Yerusalemu, nasonkhanitsa nyumba yonse ya Yuda, ndi fuko la Benjamini, ankhondo osankhika zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu, kuyambana nayo nyumba ya Israele, kubwezanso ufumu kwa Rehobowamu mwana wa Solomoni. Ndipo mau a Mulungu anafika kwa Semaya mneneri wa Mulungu, nati, Lankhula kwa Rehobowamu mwana wa Solomoni mfumu ya Yuda, ndi kwa nyumba yonse ya Yuda, ndi Benjamini, ndi kwa anthu otsalawo, nuti, Yehova atero, Musamuka, ndipo musakayambana ndi abale anu ana a Israele, bwererani yense kunyumba kwake; popeza chinthuchi chachokera kwa Ine. Ndipo iwo anamvera mau a Yehova, natembenuka, nabwerera monga mwa mau a Yehova. Ndipo Yerobowamu anamanga Sekemu m'mapiri a Efuremu, nakhalamo, natulukamo, namanga Penuwele. Ndipo Yerobowamu ananena m'mtima mwake, Ufumuwu udzabwereranso kunyumba ya Davide. Anthu awa akamakwera kukapereka nsembe m'nyumba ya Yehova m'Yerusalemu, pamenepo mitima ya anthu awa idzatembenukiranso kwa mbuye wao, kwa Rehobowamu mfumu ya Yuda; ndipo adzandipha, nadzabweranso kwa Rehobowamu mfumu ya Yuda. Potero mfumu inakhala upo, napanga anaang'ombe awiri agolide, nati kwa iwo, Kukulemetsani kukwera ku Yerusalemu; tapenyani Aisraele inu milungu yanu, imene inakutulutsani m'dziko la Ejipito. Ndipo anaimika mmodzi ku Betele, naimika wina ku Dani. Koma chinthu ichi chinasanduka tchimo, ndipo anthu ananka ku mmodziyo wa ku Dani. Iye namanga nyumba za m'misanje, nalonga anthu achabe akhale ansembe, osati ana a Levi ai. Ndipo Yerobowamu anaika madyerero mwezi wachisanu ndi chitatu, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi olingana ndi madyerero aja a ku Yuda, napereka nsembe pa guwa la nsembe; anatero m'Betele, nawaphera nsembe anaang'ombe aja anawapanga, naika m'Betele ansembe a misanje imene anaimanga. Ndipo anapereka nsembe pa guwa la nsembe analimanga m'Betele, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachisanu ndi chitatu, m'mwezi umene anaulingirira m'mtima mwa iye yekha, nawaikira ana a Israele madyerero, napereka nsembe pa guwa la nsembe, nafukiza zonunkhira. Ndipo onani, munthu wa Mulungu anachokera ku Yuda mwa mau a Yehova nadza ku Betele; ndipo Yerobowamu anali kuimirira m'mbali mwa guwa la nsembe kufukiza zonunkhira. Ndipo iye anafuula mwa mau a Yehova kutemberera guwa la nsembe, nati, Guwa la nsembe, guwa la nsembe, atero Yehova, Taona mwana adzabadwa m'nyumba ya Davide, dzina lake ndi Yosiya, adzaphera pa iwe ngati nsembe anthu ansembe a misanje, amene alikufukiza zonunkhira pa iwe, nadzatentha pa iwe mafupa a anthu. Ndipo iye anapatsa chizindikiro tsiku lomwelo, nati, Chizindikiro chimene Yehova ananena ndi ichi, Taonani guwali la nsembe lidzang'ambika, ndi phulusa lili pa ilo lidzatayika. Ndipo kunachitika, pakumva mfumu mau a munthu wa Mulungu amene anawafuula, kutemberera guwa la nsembe m'Betele, Yerobowamu anatansa dzanja lake ali ku guwalo, nati, Mgwireni iye. Ndipo dzanja lake analitansira kwa iye linauma, kuti sanathe kulifunyatitsanso. Ndiponso guwalo linang'ambika, ndi phulusa la pa guwalo linatayika, monga mwa chizindikiro chimene munthu wa Mulungu anapatsa mwa mau a Yehova. Ndipo mfumu inayankha niti kwa munthu wa Mulungu, Undipembedzere Yehova Mulungu wako, nundipempherere, kuti dzanja langa libwerenso kwa ine. Ndipo munthuyo wa Mulungu anapembedza Yehova, ndipo dzanja la mfumu linabwezedwa kwa iye momwemo mwa kale. Mfumu niti kwa munthu wa Mulungu, Tiye kwathu, ukapumule, ndikupatse mphatso. Ndipo munthu wa Mulungu ananena ndi mfumu, Mungakhale mundigawira pakati ndi pakati nyumba yanu, sindilowa kwa inu, kapena kudya mkate, kapena kumwa madzi kuno. Pakuti potero ndinalamulidwa ndi mau a Yehova, ndi kuti, Usakadye mkate, kapena kumwa madzi, kapena kubwerera njira yomweyo unadzerayo. Tsono iye anayenda njira ina osabwerera njira yomweyo anaidzera pakudza ku Betele. Ndipo ku Betele kunakhala mneneri wokalamba, ndipo mwana wake wina anadzamfotokozera machitidwe onse anawachita munthu wa Mulunguyo tsiku lomwelo m'Betele ndi mau ake anawanena ndi mfumu; inde omwe aja iwo anamfotokozera atate wao. Ndipo atate wao anati kwa iwo, Wapitira njira yiti? Popeza ana ake adaona njira analowera munthu wa Mulungu anachokera ku Yudayo. Nanena ndi ana ake, Ndimangireni mbereko pa bulu. Namangira iwo mbereko pa bulu, naberekekapo iye. Natsata munthu wa Mulungu, nampeza ali tsonga patsinde pa mtengo wathundu, nanena naye, Kodi ndiwe munthu wa Mulungu amene uja anachokera ku Yuda? Nati, Ndine amene. Tsono ananena naye, Tiye kwathu, ukadye mkate. Nati iye, Sindingabwerere nawe kukalowa kwanu, kapena kudya mkate, kapena kumwa nawe madzi pano; pakuti mau a Yehova anadza kwa ine, nati Usakadye mkate, kapena kubwerera njira yomweyo unadzerayo. Ndipo anati kwa iye, Inenso ndine mneneri wonga iwe, ndipo mthenga analankhula ndi ine mwa mau a Yehova, nati, Kambwezere kwanu, kuti akadye mkate, namwe madzi. Koma anamnamiza. Tsono anabwerera naye, nakadya kwao, namwa madzi. Ndipo kunachitika iwo ali chikhalire pagome, mau a Yehova anadza kwa mneneri amene anambwezayo, nafuula iye kwa munthu uja wa Mulungu anachokera ku Yudayo, nati, Atero Yehova Pokhala sunamvera mau a pakamwa pa Yehova, osasunga lamulo lija Yehova Mulungu wako anakulamulira, koma unabwerera nudya mkate, ndi kumwa madzi paja pomwe Iye anakuuza, Usakadye mkate, kapena kumwa madzi, mtembo wako tsono sudzaikidwa ku manda a atate ako. Ndipo kunachitika, atadya iye mkate, ndi kumwa madzi, anammangira mbereko pa bulu mneneri amene anambwezayo. Ndipo atachoka iye, mkango unakomana naye panjira, numupha ndipo mtembo wake unagwera m'njiramo, bulu naima pafupi, mkangonso unaima pafupi ndi mtembo. Ndipo onani, anthu anapitapo naona mtembo wogwera m'njiramo, ndi mkango uli chiimire pafupi ndi mtembo, nadzanena m'mudzi m'mene munakhala mneneri wokalamba uja. Ndipo mneneri amene uja anambweza panjirayo atamva, anati, Ndiye munthu uja wa Mulungu amene sanamvere mau a Yehova; chifukwa chake Yehova wampereka kwa mkango, numkadzula numupha, monga mwa mau a Yehova analankhula nayewo. Iye nanena ndi ana ake, nati, Ndimangireni mbereko pa bulu. Namangira mbereko. Namuka iye, napeza mtembo wake wogwera m'njira, ndi bulu ndi mkango zili chiimire pafupi ndi mtembo. Mkango udalibe kudya mtembo, kapena kukadzula bulu. Ndipo mneneri ananyamula mtembo wa munthu wa Mulunguyo, nausenza pa bulu, nabwera nao, nalowa m'mudzi mneneri wokalamba kumlira ndi kumuika. Ndipo mtembo wake anauika m'manda a iye mwini, namlira iwo maliro, nati, Mayo, mbale wanga! Ndipo kunachitika, atamuika iye, ananena ndi ana ake, nati, Nkadzamwalira ine mudzandiike ine m'manda momwemo mwaikidwa munthu wa Mulunguyo, ikani mafupa anga pafupi ndi mafupa ake. Popeza mau aja anawafuula mwa mau a Yehova kutemberera guwa la nsembe la ku Betele, ndi kutemberera nyumba zonse za misanje ili m'midzi ya ku Samariya, adzachitika ndithu. Pambuyo pa ichi Yerobowamu sanabwerere pa njira yake yoipa, koma analonganso anthu achabe akhale ansembe a misanje, yense wakufuna yemweyu anampatula akhale wansembe wa misanje. Ndimo umu munali tchimo la nyumba ya Yerobowamu, limene linaidula ndi kuiononga pa dziko lapansi. Nthawi yomweyo Abiya mwana wa Yerobowamu anadwala. Ndipo Yerobowamu ananena ndi mkazi wake, Unyamuke, nudzizimbaitse, ungadziwike kuti ndiwe mkazi wa Yerobowamu, nupite ku Silo; taona, kumeneko kuli Ahiya mneneri uja anandiuza ine ndidzakhala mfumu ya anthu awa. Nupite nayo mikate khumi, ndi timitanda, ndi chigulu cha uchi, numuke kwa iye; adzakuuza m'mene umo akhalire mwanayo. Natero mkazi wa Yerobowamu, nanyamuka namka ku Silo, nalowa m'nyumba ya Ahiya. Koma Ahiya sanatha kupenya, popeza maso ake anali tong'o, chifukwa cha ukalamba wake. Ndipo Yehova ananena ndi Ahiya, Taona, mkazi wa Yerobowamu akudza kukufunsa za mwana wake, popeza adwala; udzanena naye mwakutimwakuti; popeza kudzakhala pakulowa iye adzadzizimbaitsa. Ndipo kunachitika, pamene Ahiya anamva mgugu wa mapazi ake alinkulowa pakhomo, anati, Lowa mkazi iwe wa Yerobowamu, wadzizimbaitsiranji? Pakuti ine ndatumidwa kwa iwe ndi mau olasa. Kauze Yerobowamu, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Ndingakhale ndinakukulitsa pakati pa anthu, ndi kukukhalitsa pakati pa anthu ndi kukukhalitsa mfumu ya anthu anga Aisraele, ndipo ndinalanda nyumba ya Davide ufumu, ndi kuupereka kwa iwe, koma sunafanana ndi Davide mtumiki wanga uja, amene anasunga malamulo anga, nanditsata ndi mtima wake wonse kuchita zolunjika zokhazokha pamaso panga; koma wachimwa koposa onse akale, nukadzipangira milungu ina ndi mafano yoyenga kundikwiyitsa, nunditaya Ine kumbuyo kwako; chifukwa chake, taona ndidzafikitsa choipa pa nyumba ya Yerobowamu, ndi kugulula mwana wamwamuna yense wa Yerobowamu womangika ndi womasuka m'Israele, ndipo ndidzachotsa psiti nyumba yonse ya Yerobowamu, monga munthu achotsa ndowe kufikira idatha yonse. Agalu adzadya aliyense wa Yerobowamu wakufa m'mudzi; ndi mbalame za m'mlengalenga zidzadya yense wakufera kuthengo; popeza wanena ndi Yehova. Tanyamuka tsono, numuke kwanu; pakulowa mapazi ako m'mudzi mwanayo adzatsirizika. Ndipo Aisraele onse adzamlira, nadzamuika, popeza iye yekha wa ana a Yerobowamu adzalowa m'manda; pakuti mwa iye mwapezedwa chokoma cha kwa Yehova Mulungu wa Israele m'nyumba ya Yerobowamu. Ndiponso Yehova adzadziukitsira mfumu ya Israele, idzaononga nyumba ya Yerobowamu tsiku lomwelo; nchiyani ngakhale tsopano apa? Popeza Yehova adzawakantha Aisraele monga bango ligwedezeka ndi madzi, nadzazula Aisraele m'dziko lino labwino analipatsa makolo ao, nadzawamwazira ku tsidya lija la Yufurate, popeza iwo anapanga zifanizo zao zokwiyitsa Yehova. Ndipo adzapereka Aisraele chifukwa cha machimo a Yerobowamu anachimwawo, nachimwitsa nao Aisraele. Ndipo mkazi wa Yerobowamu ananyamuka nachoka, nafika ku Tiriza; ndipo polowa iye pa khomo la nyumba yake anatsirizika mwanayo. Ndipo anamuika, namlira Aisraele, monga mwa mau a Yehova anawalankhula pa dzanja la mtumiki wake Ahiya mneneri. Ndipo machitidwe ena a Yerobowamu m'mene umo anachitira ufumu, taona, analembedwa m'buku la machitidwe a mafumu a Israele. Ndipo masiku akukhala Yerobowamu mfumu anali zaka makumi awiri mphambu ziwiri, nagona iye ndi makolo ake, nalowa ufumu m'malo mwake Nadabu mwana wake. Ndipo Rehobowamu mwana wa Solomoni anali mfumu ya dziko la Yuda. Rehobowamu anali wa zaka makumi anai mphambu chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri m'Yerusalemu, m'mudzi m'mene Yehova adausankha m'mafuko onse a Israele kukhazikamo dzina lake. Ndipo dzina la amake linali Naama Mwamoni. Ndipo Ayuda anachita zoipa pamaso pa Yehova, namchititsa nsanje ndi zoipa zao anazichitazo, zakuposa zija adazichita makolo ao. Pakuti anadzimangiranso misanje, ndi zoimiritsa, ndi zifanizo, pa chitunda chonse chachitali, ndi patsinde pa mtengo wogudira uliwonse; panalinso anyamata ochitirana dama m'dzikomo; iwo amachita monga mwa zonyansitsa za amitundu, amene Yehova anapirikitsa pamaso pa ana a Israele. Ndipo kunachitika, Rehobowamu atakhala mfumu zaka zisanu, Sisake mfumu ya Aejipito anakwera ndi nkhondo ku Yerusalemu, nachotsa chuma cha m'nyumba ya Yehova, ndi chuma cha m'nyumba ya mfumu; inde anachotsa chonsecho, nachotsanso zikopa zagolide zonse adazipanga Solomoni. Ndipo mfumu Rehobowamu anapanga m'malo mwa izo zikopa zina zamkuwa, nazipereka m'manja a akapitao a olindirira, akusunga pakhomo pa nyumba ya mfumu. Ndipo kunachitika, pakulowa mfumu m'nyumba ya Yehova, olindirira aja anazinyamula, nabweranso nazo ku chipinda cha olindirirawo. Tsono, machitidwe ake ena a Rehobowamu, ndi zonse anazichita, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda? Ndipo panali nkhondo pakati pa Rehobowamu ndi Yerobowamu masiku ao onse. Nagona Rehobowamu ndi makolo ake, naikidwa kwa makolo ake m'mudzi wa Davide. Ndipo dzina la amake linali Naama Mwamoni, nalowa ufumu m'malo mwake Abiya mwana wake. Ndipo chaka chakhumi mphambu zisanu ndi zitatu cha mfumu Yerobowamu mwana wa Nebati, Abiya analowa ufumu wa Yuda. Anakhala mfumu zaka zitatu m'Yerusalemu, ndipo dzina la amake linali Maaka mwana wa Abisalomu. Nayenda iye m'zoipa zonse za atate wake, zimene iye adachita asanalowe ufumu Abiyayo; ndipo mtima wake sunali wangwiro ndi Yehova Mulungu wake monga mtima wa Davide kholo lake. Koma chifukwa cha Davideyo Yehova Mulungu wake anampatsa nyali m'Yerusalemu, kumuikira mwana wake pambuyo pake, ndi kukhazikitsa Yerusalemu; chifukwa kuti Davide adachita cholungama pamaso pa Yehova, osapatuka masiku ake onse pa zinthu zonse adamlamulira Iye, koma chokhacho chija cha Uriya Muhiti. Ndipo panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobowamu masiku onse a moyo wake. Ndipo machitidwe ake ena a Abiya, ndi zonse anazichita, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda? Ndipo panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobowamu. Nagona Abiya ndi makolo ake, namuika anthu m'mudzi wa Davide; Asa mwana wake nalowa ufumu m'malo mwake. Ndipo chaka cha makumi awiri cha Yerobowamu mfumu ya Israele, Asa anayamba kukhala mfumu ya Yuda. Nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi anai mphambu chimodzi, ndipo dzina la amake linali Maaka mwana wa Abisalomu. Ndipo Asa anachita zabwino pamaso pa Yehova monga Davide kholo lake. Nachotsa m'dziko anyamata aja adama, nachotsanso mafano onse anawapanga atate ake. Ndipo anamchotsera Maaka amake ulemu wa make wa mfumu, popeza iye anapanga fanizo lolaula; ndipo Asa analikha fano lake, nalitentha ku mtsinje wa Kidroni. Koma misanje sanaichotse, koma mtima wa Asa unali wangwiro ndi Yehova masiku ake onse. Ndipo analonga m'nyumba ya Yehova zinthu zija atate wake adazipereka; napereka zinthu zina iye mwini zasiliva ndi zagolide ndi zotengera. Ndipo panali nkhondo pakati pa Asa ndi Baasa mfumu ya Israele masiku ao onse. Ndipo Baasa mfumu ya Israele anakwera ndi nkhondo ku Yuda, namanga ku Rama kuwaletsa anthu asatuluke kapena kulowa kwa Asa mfumu ya Yuda. Tsono Asa anatenga siliva yense ndi golide yense anatsala pa chuma cha nyumba ya Yehova, ndi chuma chili m'nyumba ya Yehova chuma chili m'nyumba ya mfumu, nazipereka m'manja mwa anyamata ake; ndipo mfumu Asa anazitumiza kwa Benihadadi mwana wa Tabirimoni, mwana wa Heziyoni mfumu ya Aramu, wakukhala ku Damasiko, nati, Pakhale pangano pakati pa ine ndi inu, pakati pa atate wanga ndi atate wanu; taonani, ndatumiza kwa inu mphatso ya siliva ndi golide, tiyeni lilekeke pangano lili pakati pa inu ndi Baasa mfumu ya Israele, kuti andichokere. Ndipo Benihadadi anamvera mfumu Asa, natuma akazembe a nkhondo ake kukathira nkhondo kumidzi ya Israele, napasula Iyoni, ndi Dani, ndi Abele-Beti-Maaka, ndi Kineroti wonse, ndi dziko lonse la Nafutali. Tsono Baasa atamva izi, analeka kumanga ku Rama nakhala pa Tiriza. Pamenepo mfumu Asa anamemeza Ayuda onse, osatsala ndi mmodzi yense; natuta miyala ya ku Rama, ndi mitengo yomwe, akamange nayo Baasa; ndi mfumu Asa anamangira Geba wa ku Benjamini, ndi Mizipa. Ndipo machitidwe onse ena a Asa, ndi mphamvu yake yonse, ndi zonse anazichita, ndi midzi anaimanga, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda? Koma masiku a ukalamba wake anadwala mapazi ake. Nagona Asa ndi makolo ake, naikidwa kwa makolo ake m'mudzi wa Davide kholo lake; ndipo Yehosafati mwana wake analowa ufumu m'malo mwake. Ndipo Nadabu mwana wa Yerobowamu analowa ufumu wa Israele chaka chachiwiri cha Asa mfumu ya Yuda, nakhala mfumu ya Israele zaka ziwiri. Nachita zoipa pamaso pa Yehova, nayenda m'njira ya atate wake, ndi m'tchimo lomwelo iye akachimwitsa nalo Aisraele. Ndipo Baasa mwana wa Ahiya, wa nyumba ya Isakara, anampangira chiwembu; ndipo Baasa anamkanthira ku Gibetoni wa Afilisti, popeza Nadabu ndi Aisraele onse adamangira misasa Gibetoni. Inde Baasa anamupha chaka chachitatu cha Asa mfumu ya Yuda, nalowa ufumu m'malo mwake. Tsono kunachitika, pokhala mfumu iye, anakantha nyumba yonse ya Yerobowamu, kufikira adamuononga monga mwa mau a Yehova, amene analankhula pa dzanja la mtumiki wake Ahiya wa ku Silo; chifukwa cha machimo a Yerobowamu, amene adachimwa nao, nachimwitsa nao Aisraele, ndi kuutsa kwake kumene anaputa nako mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israele. Ndipo machitidwe ena a Nadabu, ndi zonse anazichita, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele? Ndipo panali nkhondo pakati pa Asa ndi Baasa mfumu ya Israele masiku ao onse. Tsono Baasa mwana wa Ahiya analowa ufumu wa Israele chaka chachitatu cha Asa mfumu ya Yuda, nakhala mfumu ku Tiriza zaka makumi awiri mphambu zinai. Ndipo anachimwa pamaso pa Yehova, nayenda m'njira ya Yerobowamu, ndi m'tchimo lake iye anachimwitsa nalo Israele. Ndipo mau a Yehova akutsutsa Baasa anadza kwa Yehu mwana wa Hanani, nati, Popeza ndinakukuza iwe kuchokera kufumbi, ndi kukuika iwe mfumu ya anthu anga Israele, koma iwe unayenda m'njira ya Yerobowamu, ndi kuchimwitsa anthu anga Israele, kuputa mkwiyo wanga ndi machimo ao; taona, ndidzachotsa psiti Baasa ndi nyumba yake, ndipo ndidzafanizitsa nyumba yako ndi nyumba ya Yerobowamu mwana wa Nebati, Agalu adzadya aliyense wa Baasa amene adzafera m'mudzi, ndipo amene adzafera m'thengo zidzamudya mbalame za m'mlengalenga. Tsono machitidwe ena a Baasa, ndi ntchito zake, ndi mphamvu zake, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele? Nagona Baasa ndi makolo ake, naikidwa ku Tiriza; ndipo Ela mwana wake analowa ufumu m'malo mwake. Ndiponso mau a Yehova anadza ndi dzanja la mneneri Yehu mwana wa Hanani, kutsutsa Baasa ndi nyumba yake, chifukwa cha zoipa zonse anazichita iye pamaso pa Yehova; popeza anaputa mkwiyo wake ndi machitidwe a manja ake, nafanana ndi nyumba ya Yerobowamu; ndiponso popeza anaikantha. Ndipo chaka cha makumi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi cha Asa mfumu ya Yuda, Ela mwana wa Baasa analowa ufumu wa Israele ku Tiriza, nakhala mfumu zaka ziwiri. Ndipo mnyamata wake Zimiri, ndiye woyang'anira dera lina la magaleta ake, anampangira chiwembu; koma iye anali m'Tiriza kumwa ndi kuledzera m'nyumba ya Ariza, ndiye woyang'anira nyumba m'Tiriza. Nalowamo Zimiri, namkantha, namupha chaka cha makumi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri za Asa mfumu ya Yuda, nalowa ufumu m'malo mwake. Ndipo kunali, atalowa ufumu wake, nakhala pa mpando wachifumu wake, anawakantha onse a m'nyumba ya Baasa, osamsiyira mwana wamwamuna ndi mmodzi yense, kapena wa abale ake, kapena wa mabwenzi ake. Motero Zimiri anaononga nyumba yonse ya Baasa, monga mwa mau a Yehova, amene ananena akumtsutsa Baasa, mwa dzanja la Yehu mneneri, chifukwa cha machimo onse a Baasa, ndi machimo a Ela mwana wake anachimwawo, nachimwitsa nao Aisraele, kuputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israele ndi zachabe zao. Tsono machitidwe ena a Ela, ndi ntchito zake zonse, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele? Ndipo chaka cha makumi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri cha Asa mfumu ya Yuda, Zimiri anali mfumu masiku asanu ndi awiri ku Tiriza. Ndipo anthu analikumangira misasa Gibetoni wa Afilisti. Koma anthu aja omangira misasa anamva kuti Zimiri wachita chiwembu, nakanthanso mfumu; chifukwa chake tsiku lomwelo Aisraele onse a kumisasa anamlonga Omuri kazembe wa nkhondo akhale mfumu ya Israele. Ndipo Omuri anachoka ku Gibetoni, ndi Aisraele onse naye, nakamangira misasa Tiriza. Kunali tsono, pakuona Zimiri kuti nkhondo yalowa m'mudzi, anakwera pa nsanja ya nyumba ya mfumu, nadzitenthera ndi moto nyumba ya mfumu, nafa; chifukwa cha machimo ake anachimwawo, pakuchita choipa pamaso pa Yehova; popeza anayenda m'njira ya Yerobowamu, ndi m'tchimo lake anachimwa nalolo, nachimwitsa nalo Aisraele. Machitidwe ena tsono a Zimiri, ndi chiwembu anachichitacho, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele? Pamenepo anthu a Israele anagawika pakati, anthu ena anatsata Tibini mwana wa Ginati kumlonga ufumu, ena natsata Omuri. Koma anthu akutsata Omuri anapambana iwo akutsata Tibini mwana wa Ginati; nafa Tibini, Omuri nakhala mfumu. Chaka cha makumi atatu ndi chimodzi cha Asa mfumu ya Yuda, Omuri anayamba kukhala mfumu ya Israele, nakhala zaka khumi ndi ziwiri; ku Tiriza anali mfumu zaka zisanu ndi chimodzi. Ndipo anagula kwa Semeri chitunda cha Samariya ndi matalente awiri a siliva, namanga pachitundapo, natcha dzina lake la mudzi anaumanga Samariya, monga mwa dzina la Semeri mwini chitundacho. Koma Omuri anachimwa pamaso pa Yehova, nachita zoipa koposa onse adamtsogolerawo. Nayenda m'njira yonse ya Yerobowamu mwana wa Nebati, ndi tchimo lake anachimwitsa nalo Aisraele, kuputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israele ndi zachabe zao. Ndipo machitidwe ena a Omuri anawachita, ndi mphamvu yake anaionetsa, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele? Nagona Omuri ndi makolo ake, naikidwa m'Samariya; ndipo Ahabu mwana wake analowa ufumu m'malo mwake. Ndipo chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu cha Asa mfumu ya Yuda Ahabu mwana wa Omuri analowa ufumu wa Israele, nakhala Ahabu mwana wa Omuri mfumu ya Israele m'Samariya zaka makumi awiri mphambu ziwiri. Ndipo Ahabu mwana wa Omuri anachimwa pamaso pa Yehova koposa onse adamtsogolerawo. Ndipo kunali monga ngati kunamchepera kuyenda m'machimo a Yerobowamu mwana wa Nebati, iye anakwatira Yezebele mwana wamkazi wa Etibaala mfumu ya Asidoni, natumikira Baala, namgwadira. Nammangira Baala guwa la nsembe m'nyumba ya Baala anaimanga m'Samariya. Ahabu anapanganso chifanizo; ndipo Ahabu amene anapambana mafumu onse a Israele adamtsogolerawo, kuputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israele. M'masiku ake Hiyele wa ku Betele anamanga Yeriko; pokhazika maziko ake anadzifetsera Abiramu mwana wake woyamba, poimika zitseko zake anadzifetsera Segubu mwana wake wotsiriza; monga mwa mau a Yehova amene ananenetsa Yoswa mwana wa Nuni. Ndipo Eliya wa ku Tisibe wokhala ku Giliyadi ananena ndi Ahabu, nati, Pali Yehova Mulungu wa Israele, amene ndimakhala pamaso pake, ngati adzagwa mame kapena mvula zaka izi, koma ntanena ine ndipo. Ndipo mau a Yehova anadza kwa iye, nati, Choka kuno, nutembenukire kum'mawa, ukabisale kumtsinje Keriti uli ku Yordani. Ndipo kudzakhala kuti uzikamwa mumtsinje, ndipo ndalamulira makungubwi kukudyetsa kumeneko. Momwemo iye anamuka, nachita monga mwa mau a Yehova, nakakhala kumtsinje Keriti uli ku Yordani. Ndipo makungubwi anamtengera mkate ndi nyama m'mawa, ndi mkate ndi nyama madzulo; namamwa iye mumtsinje. Ndipo kunachitika, atapita masiku ena mtsinje udaphwa, popeza munalibe mvula m'dziko. Ndipo mau a Yehova anadza kwa iye, nati, Nyamuka, pita ku Zarefati wa ku Sidoni, nukhale kumeneko; taona, ndamlamulira mkazi wamasiye wa kumeneko akudyetse. Tsono iye ananyamuka namka ku Zarefati, nafika ku chipata cha mudzi; ndipo taona mkazi wamasiye anali kutola nkhuni; ndipo iye anamuitana, nati, Unditengere madzi pang'ono m'chikho, ndimwe. Ndipo m'mene analikumuka kukatenga iye anamuitananso, nati, Unditengerenso kanthongo ka mkate m'dzanja lako. Nati iye, Pali Yehova Mulungu wako, ndilibe mkate, koma kaufa dzanja limodzi kali m'mbiya, ndi mafuta pang'ono m'nsupa; ndipo taona, ndilikutola nkhuni ziwiri kuti ndikadziphikire ndekha ndi mwana wanga, tidye, tife. Ndipo Eliya anati kwa iye, Usachita mantha, kachite monga umo wanenamo, koma thanga wandiocherako kamkate, nubwere nako kwa ine; ndipo utatero udziphikire wekha ndi mwana wako. Popeza atero Yehova Mulungu wa Israele, Mbiya ya ufa siidzatha, ndipo nsupa ya mafuta siidzachepa, kufikira tsiku lakugwetsa mvula Yehova pa dziko lapansi. Ndipo iye anakachita monga mwa mau a Eliya, nadya iye mwini, ndi iyeyo, ndi a m'nyumba ake, masiku ambiri. Mbiya ya ufa siidatha, ndi nsupa ya mafuta siinachepa, monga mwa mau a Yehova amene ananenetsa Eliya. Ndipo kunali, zitatha izi, mwana wa mkazi mwini nyumbayo anadwala; ndipo pokula nthenda yake, analeka kupuma. Ndipo mkaziyo ananena ndi Eliya, Ndili nawe chiyani munthu iwe wa Mulungu? Kodi wadza kwa ine kundikumbutsa tchimo langa, ndi kundiphera mwana wanga? Ndipo ananena naye, Ndipatse mwana wako. Namtenga m'mfukato mwake napita naye ku chipinda chosanja chogonamo iyeyo, namgoneka pa kama wa iye mwini. Nafuulira kwa Yehova, nati, Yehova Mulungu wanga, kodi mwamgwetsera choipa mkazi wamasiye amene ndikhala naye, kumphera mwanake? Nafungatira katatu pa mwanayo, nafuulira kwa Yehova, nati, Yehova Mulungu wanga, ndikupemphani, ubwere moyo wake wa mwanayu m'chifuwa mwake. Ndipo Yehova anamva mau a Eliya, ndipo moyo wa mwanayo unalowanso mwa iye, nakhalanso moyo. Ndipo Eliya ananyamula mwanayo, natsika naye ku chipinda chosanja, nalowa naye m'nyumba, nampereka kwa amake; nati, Eliya, Taona, mwana wako ali moyo. Ndipo mkazi anati kwa Eliya, Ndizindikira tsopano kuti ndinu munthu wa Mulungu, ndi kuti mau a Yehova ali m'kamwa mwanuwo ngoona. Ndipo atapita masiku ambiri, mau a Yehova anafika kwa Eliya chaka chachitatu, nati, Kadzionetse kwa Ahabu, ndipo ndidzatumiza mvula padziko. Ndipo Eliya ananka kukadzionetsa kwa Ahabu. Ndipo njala inali yaikulu m'Samariya. Ndipo Ahabu anaitana Obadiya woyang'anira nyumba yake. Koma Obadiya anaopa ndithu Yehova; pakuti pamene Yezebele anapulula aneneri a Yehova, Obadiya anatenga aneneri zana limodzi, nawabisa makumi asanuasanu m'phanga, nawadyetsa mkate ndi madzi. Ndipo Ahabu anati kwa Obadiya, Kayendere dziko lonse ku zitsime zonse zamadzi, ndi ku mitsinje yonse, kapena tikapeza msipu ndi kusunga moyo wa akavalo ndi nyuru, zingafe nyama zonse. Tsono iwo awiri anagawana dziko kukaliyendera; Ahabu anadzera njira yake yekha, ndi Obadiya njira ina yekha. Ndipo Obadiya ali m'njira taona, Eliya anakomana naye; iye namdziwa, namgwadira, nati, Ndinu kodi mbuye wanga Eliya? Ndipo anamyankha, nati, Ndine amene; kauze mbuye wako kuti Eliya wabwera. Iye nati, Ndachimwanji kuti mupereka kapolo wanu m'dzanja la Ahabu kundipha? Pali Yehova Mulungu wanu, ngati kuli mtundu umodzi wa anthu, kapena ufumu, kumene mbuye wanga sananditumeko kukufunani, ndipo pakunena iwo, Palibe iye, analumbiritsa ufumu umene ndi mtundu umene kuti sanakupezeni. Ndipo tsopano mukuti, Kauze mbuye wako kuti Eliya wabwera. Ndipo kudzachitika, ine ntakusiyani, mzimu wa Yehova udzakunyamulirani kosakudziwa ine, ndipo ine ntakauza Ahabu, ndipo akalephera kukupezani, adzandipha. Koma ine kapolo wanu ndimaopa Yehova kuyambira ubwana anga. Kodi sanakuuzeni mbuye wanga chimene ndidachita m'kuwapha Yezebele aneneri a Yehova, kuti ine ndidabisa aneneri a Yehova zana limodzi makumi asanuasanu m'phanga, ndi kuwadyetsa mkate ndi madzi? Ndipo tsopano inu mukuti, Kauze mbuye wako Eliya wabwera, ndipo adzandipha. Koma Eliya anati, Pali Yehova wa makamu, amene ndikhala pamaso pake, zedi, ndionekadi pamaso pake lero. Ndipo Obadiya anauka kukomana ndi Ahabu, namuuza, ndipo Ahabu ananka kukomana ndi Eliya. Ndipo kunachitika pamene Ahabu anaona Eliya, Ahabu anati kwa iye, Kodi ndiwe uja umavuta Israeleyo? Nati iye, Sindimavuta Israele ine ai, koma inu ndi nyumba ya atate wanu; popeza munasiya malamulo a Yehova, ndi kutsata Abaala. Ndipo tsono, tumani mundimemezere Aisraele onse kuphiri la Karimele, ndi aneneri a Baala mazana anai mphambu makumi asanu, ndi aneneri a chifanizocho mazana anai, akudya pa gome la Yezebele. Pamenepo Ahabu anatumiza mau kwa ana onse a Israele, namemeza aneneri onse kuphiri la Karimele. Ndipo Eliya anayandikira kwa anthu onse, nati, Mukayikakayika kufikira liti? Ngati Yehova ndiye Mulungu, mtsateni Iye; ngati Baala, mumtsate iyeyo. Ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe anamuyankha. Ndipo Eliya ananena ndi anthuwo, Ine ndatsala ndekha mneneri wa Yehova, koma aneneri a Baala ndiwo anthu mazana anai mphambu makumi asanu. Atipatse tsono ng'ombe ziwiri; ndipo adzisankhire iwo eni ng'ombe imodzi, naiduledule, naiike pankhuni osasonkhapo moto; ndipo ine ndidzakonza ng'ombe yinayo, ndi kuiika pankhuni osasonkhapo moto. Ndipo muitane inu dzina la mulungu wanu, ine ndidzaitana dzina la Yehova; ndipo Mulunguyo ayankhe ndi moto ndiye Mulungu. Ndipo anthu onse anavomera, nati, Ndiwo mau abwino amene. Pamenepo Eliya ananena ndi aneneri a Baala, Dzisankhireni ng'ombe imodzi yanu, muyambe kuikonza, popeza muchuluka; nimuitane dzina la mulungu wanu, koma musasonkhepo moto. Ndipo iwo anatenga ng'ombe ija adawapatsa, naikonza, naitana dzina la Baala, kuyambira m'mawa kufikira pausana, nati, Baala, timvereni ife. Koma panalibe mau kapena wovomereza. Ndipo anavinavina kuguwa adalimanga. Ndipo pausana Eliya anawaseka, nati, Kwezani mau, popeza ndiye mulungu; kapena alikulingirira, kapena wapambuka, kapena ali paulendo, kaya agona, adzagalamuka. Ndipo anakwezadi mau, nadzitema monga makhalidwe ao ndi mipeni ndi nthungo, kuti mwazi wao unali chuchuchu. Ndipo kunali, litapendeka dzuwa, ananenera kufikira nthawi ya kupereka nsembe; koma panalibe mau, kapena wovomereza, kapena wakuwamvera. Pamenepo Eliya ananena ndi anthu onse, Senderani kwa ine; ndipo onse anasendera kwa iye. Iye nakonza guwa la nsembe la Yehova lidagumukalo. Ndipo Eliya anatenga miyala khumi ndi iwiri, monga mwa ziwerengo cha mafuko ana a Yakobo, amene mau a Yehova adamfikira, kuti, Dzina lako ndi Israele. Ndipo ndi miyalayi anamanga guwa la nsembe m'dzina la Yehova, nazunguniza guwalo ndi mchera, ukulu wake ngati kulandira miyeso iwiri ya mbeu kuzinga guwalo. Ndipo anakonza nkhunizo, naduladula ng'ombe, naiika pankhuni. Nati, Dzazani madzi mbiya zinai, muwathire pa nsembe yopsereza ndi pankhuni. Nati, Bwerezaninso kawiri; nabwerezanso. Nati, Bwerezani katatu; nabwereza katatu. Ndipo madzi anayenda pozinga guwa la nsembe, nadzazanso mcherawo ndi madzi. Ndipo kunali, nthawi ya kupereka nsembe yamadzulo, Eliya mneneri anasendera, nati, Yehova Mulungu wa Abrahamu ndi Isaki ndi Israele, lero kudziwike kuti Inu ndinu Mulungu wa Israele, ndi ine mtumiki wanu, kuti mwa mau anu ndachita zonsezi. Ndimvereni Yehova, ndimvereni, kuti anthu awa adziwe kuti Inu Yehova ndinu Mulungu, ndi kuti Inu mwabwezanso mitima yao. Pamenepo moto wa Yehova unagwa, nutentha nsembe yopsereza, ndi nkhuni, ndi miyala, ndi fumbi, numwereretsa madzi anali mumchera. Ndipo anthu onse anaona, nagwa nkhope zao pansi, nati, Yehova ndiye Mulungu, Yehova ndiye Mulungu. Ndipo Eliya anati kwa iwo, Gwirani aneneri a Baala, asapulumuke ndi mmodzi yense. Nawagwira, ndipo Eliya anapita nao ku mtsinje wa Kisoni, nawapha pamenepo. Ndipo Eliya ananena ndi Ahabu, Nyamukani, idyani, imwani; popeza kumveka mkokomo wa mvula yambiri. Ndipo Ahabu anakadya, namwa; koma Eliya anakwera pamwamba pa Karimele, nagwadira pansi, naika nkhope yake pakati pa maondo ake. Ndipo anati kwa mnyamata wake, Kwera kapenyerere kunyanja. Iye nakwera, napenyetsetsa, nati, Kulibe kanthu. Nati, Bwerezanso kasanu ndi kawiri. Ndipo kunali kachisanu ndi chiwiri anati, Taonani, kwatuluka kunyanja kamtambo konga dzanja la munthu. Nati iye, Kauze Ahabu, kuti, Mangani galeta, tsikani, mvula ingakutsekerezeni. Ndipo kunali, polinda kanthawi, thambo linada ndi mitambo ndi mphepo, nigwa mvula yaikulu. Ndipo Ahabu anayenda m'galeta, namuka ku Yezireele. Ndipo dzanja la Yehova linakhala pa Eliya; namanga iye za m'chuuno mwake, nathamanga m'tsogolo mwa Ahabu ku chipata cha Yezireele. Ndipo Ahabu anauza Yezebele zonse anazichita Eliya, ndi m'mene anawaphera ndi lupanga aneneri onsewo. Tsono Yezebele anatuma mthenga kwa Eliya, wakuti, Milungu indilange nionjezepo, ngati sindilinganiza moyo wako ndi moyo wa mmodzi wa iwowo mawa nthawi yomwe yino. Ndipo iye ataona chimenechi, ananyamuka, nathawa kupulumutsa moyo, nafika ku Beereseba wa ku Yuda, nasiya mnyamata wake pamenepo. Koma iye mwini analowa m'chipululu ulendo wa tsiku limodzi, nakakhala pansi patsinde pa mtengo watsanya, napempha kuti afe; nati, Kwafikira, chotsani tsopano moyo wanga, Yehova; popeza sindili wokoma woposa makolo anga. Ndipo anagona tulo patsinde pa mtengo watsanya; ndipo taonani, wamthenga anamkhudza, nati kwa iye, Uka nudye. Ndipo anacheuka, naona kumutu kunali kamkate kootcha pamakala, ndi mkhate wa madzi. Tsono anadya namwa, nagonanso pansi. Ndipo mthenga wa Yehova anafikanso kachiwiri, namkhudza, nati, Tauka, idya, popeza ulendo udzakulaka. Tsono anauka, nadya namwa, nayenda ndi mphamvu ya chakudya chimenecho masiku makumi anai usana ndi usiku, nafika kuphiri la Mulungu ku Horebu. Nafika kuphanga, nagona kumeneko, ndipo taonani, mau a Yehova anamfikira, nati kwa iye, Uchitanji pano, Eliya? Ndipo anati, Ine ndinachitira changu Yehova Mulungu wa makamu; popeza ana a Israele anasiya chipangano chanu, napasula maguwa anu a nsembe, napha aneneri anu ndi lupanga, ndipo ndatsala ndekha, ndipo afuna moyo wanga kuuchotsa. Ndipo Iye anati, Tuluka, nuime pa phiri lino pamaso pa Yehova. Ndipo taonani, Yehova anapitapo, ndi mphepo yaikulu ndi yamphamvu inang'amba mapiri, niphwanya matanthwe pamaso pa Yehova; koma Yehova sanakhale m'mphepomo. Itapita mphepoyo kunali chivomezi; komanso Yehova sanali m'chivomezicho. Chitaleka chivomezi panali moto; koma Yehova sanali m'motomo. Utaleka moto panali bata la kamphepo kayaziyazi. Ndipo atamva Eliya, anafunda nkhope yake ndi chofunda chake, natuluka, naima pa khomo la phangalo. Ndipo taonani, anamdzera mau akunena naye, Uchitanji kuno, Eliya? Nati iye, Ndachitira changu Yehova Mulungu wa makamu; popeza ana a Israele ataya chipangano chanu, nagumula maguwa la nsembe anu, napha aneneri anu ndi lupanga; ndipo ndatsala ndekha, ndipo afuna moyo wanga kuuchotsa. Ndipo Yehova anati kwa iye, Bwerera ulendo wako, udzere kuchipululu kunka ku Damasiko, ndipo utafikako udzoze Hazaele akhale mfumu ya Aramu; ukadzozenso Yehu mwana wa Nimisi akhale mfumu ya Israele; ukadzozenso Elisa mwana wa Safati wa ku Abele-Mehola akhale mneneri m'malo mwako. Ndipo kudzachitika Yehu adzamupha amene adzapulumuka ku lupanga la Hazaele; ndi Elisa adzamupha amene adzapulumuka ku lupanga la Yehu. Ndiponso ndidasiya m'Israele anthu zikwi zisanu ndi ziwiri osagwadira Baala maondo ao, osampsompsona ndi milomo yao. Tsono anachokako, napeza Elisa mwana wa Safati alikukoketsa chikhasu ng'ombe ziwiriziwiri magoli khumi ndi awiri, iye yekha anakhala pa goli lakhumi ndi chiwiri; ndipo Eliya ananka kunali iyeyo, naponya chofunda chake pa iye. Ndipo iye anasiya ng'ombe zija, namthamangira Eliya, nati, Ndiloleni ndithange ndakampsompsona atate wanga ndi amai wanga; nditatero ndidzakutsatani. Nati iye, Bwerera ndakuchitanji? Ndipo anabwerera panali iye uja, natengako ng'ombe ziwiri, nazipha, naphikira nyama yake ndi zipangizo za zochitira nazo ng'ombe, napatsa anthu adye. Atatero, ananyamuka, natsata Eliya, namtumikira. Ndipo Benihadadi mfumu ya Aramu anamemeza khamu lake lonse la nkhondo; ndi mafumu makumi atatu mphambu awiri anali naye, pamodzi ndi akavalo ndi magaleta; nakamangira Samariya misasa, naponyana nao nkhondo. Natumiza mithenga kumudzi kwa Ahabu mfumu ya Israele, nati kwa iye, Atero Benihadadi, Siliva wako ndi golide wako ndi wanga, akazi ako ndi ana ako omwe okometsetsawo ndi anga. Ndipo mfumu ya Israele anayankha, nati, Monga mwanena, mbuye wanga mfumu, ndine wanu ndi zonse ndili nazo. Tsono mithenga ija inabwerera, niti, Atero Benihadadi, kuti, Ndinatumadi kwa iwe, ndi kuti, Uzindipatsa siliva wako, ndi golide wako, ndi akazi ako, ndi ana ako; koma mawa dzuwa lino ndidzatuma anyamata anga kwa iwe, nadzafunafuna m'nyumba mwako, ndi m'nyumba za anyamata ako; ndipo kudzakhala kuti chifuniro chonse cha maso ako adzachigwira ndi manja ao, nadzachichotsa. Pamenepo mfumu ya Israele anaitana akulu onse a dziko, nati, Tazindikirani inu, penyani kuti munthu uyu akhumba choipa; popeza anatuma kwa ine kulanda akazi anga, ndi ana anga, ndi siliva, ndi golide wanga; ndipo sindinamkaniza. Ndipo akulu onse ndi anthu onse anati kwa iye, Musamvere, musavomereze. Ndipo anati kwa mithenga ya Benihadadi, Kauzeni mbuye wanga mfumu, Zonse munayamba mundituma mtumiki wanu kuzifunsa ndidzachita, koma ichi sindingachichite. Nichoka mithengayo, nimbwezera mau. Ndipo Benihadadi anatuma kwa iye, nati, Milungu indilange, nionjezepo, ngati fumbi la Samariya lidzafikira kudzaza manja a anthu onse akutsata mapazi anga. Ndipo mfumu ya Israele anayankha, nati, Kamuuzeni, Wakumanga zida asadzikuze ngati wakuvulayo. Ndipo kunachitika, atamva Benihadadi mau awa, analikumwa nao mafumu m'misasa, ananena ndi anyamata ake, Nikani. Nandandalika pamudzipo. Ndipo taonani, mneneri anadza kwa Ahabu mfumu ya Israele, nati, Atero Yehova, Kodi waona unyinji uwu waukulu wonse? Taonani, ndidzaupereka m'dzanja mwako lero, kuti udziwe kuti ndine Yehova. Nati Ahabu, Mwa yani? Nati, Atero Yehova, Mwa anyamata a akalonga a madera. Natinso, Adzayamba kuponya nkhondo ndani? Nati, Iwe. Pamenepo anawerenga anyamata a akalonga a madera, nawapeza mazana awiri mphambu makumi atatu kudza awiri. Pamenepo anawerenganso anthu onse, ndiwo ana a Israele onse zikwi zisanu ndi ziwiri. Ndipo amenewo anatuluka usana. Koma Benihadadi analinkumwa naledzera m'misasamo, iye ndi mafumu aja makumi atatu mphambu awiri aja akumthandiza. Ndipo anyamata a akalonga a madera anayamba kutuluka, koma Benihadadi anatuma anthu, iwo nambwezera mau, kuti, M'Samariya mwatuluka anthu. Nati iye, Chinkana atulukira mumtendere, agwireni amoyo; chinkana atulukira m'nkhondo, agwireni, amoyo. Tsono anatuluka m'mudzi anyamata a akalonga a madera aja, ndi khamu la nkhondo linawatsata. Ndipo aliyense anapha munthu wake; ndipo Aaramu anathawa, Aisraele nawapirikitsa; ndipo Benihadadi mfumu ya Aramu anathawira pa kavalo pamodzi ndi apakavalo. Tsono mfumu ya Israele inatuluka, nikantha apakavalo ndi apamagaleta, nawapha Aaramuwo maphedwe akulu. Ndipo mneneri uja anayandikira kwa mfumu ya Israele, nati kwa iye, Kadzilimbitseni, mudziwe muchenjere ndi chimene muchichita; popeza chaka chikudzachi mfumu ya Aramu idzabweranso kulimbana nanu. Ndipo anyamata a mfumu ya Aramu anati kwa iye, Milungu yao nja kumapiri, ndimo m'mene atilakira; koma tikaponyana nao kuchidikha, zedi tidzaposa mphamvu. Tsono chitani ichi, chotsani mafumu aja yense ku malo ake, muike m'malo mwao akazembe. Ndipo mudziwerengere khamu la nkhondo longa khamu lija lidaonongekalo, ndi akavalo onga akavalo aja, ndi magaleta monga omwe aja; ndipo tikaponyane nao pachidikha tidzawapambana ndithu. Namvera iye mau ao, natero kumene. Tsono kunachitika, pakufikanso chaka Benihadadi anamemeza Aaramu nakwera ku Afeki kukaponyana ndi Aisraele. Ndipo Aisraele anamemezananso, anali naye kamba, nakakomana nao; ndipo Aisraele anamanga misasa yao pandunji pao, ngati timagulu tiwiri ta anaambuzi; koma Aaramu anadzaza dziko. Ndipo munthu uja wa Mulungu anafikako, nalankhula ndi mfumu ya Israele, nati, Atero Yehova, Popeza Aaramu amati, Yehova ndiye Mulungu wa kumapiri, osati Mulungu wa kuzigwa, mwa ichi ndidzapereka unyinji uwu waukulu m'dzanja mwako, kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova. Ndipo awa anakhala m'misasa pandunji pa ajawo masiku asanu ndi awiri. Tsono kunali, tsiku lachisanu ndi chiwiri anayambana nkhondo; ndipo ana a Israele anaphako Aaramu tsiku limodzi anthu oyenda pansi zikwi zana limodzi. Ndipo otsalawo anathawira ku Afeki kumudzi, ndipo linga linawagwera anthu zikwi makumi awiri mphambu asanu ndi awiri amene adatsalawo. Ndipo Benihadadi anathawa, nalowa m'mudzi, m'chipinda cha m'katimo. Pamenepo anyamata ake anati kwa iye, Taonani, tidamva ife kuti mafumu a nyumba ya Israele ndi mafumu achifundo; tiyeni tivale chiguduli m'chuuno mwathu, ndi zingwe pamitu pathu, titulukire kwa mfumu ya Israele, kapena adzakusungirani moyo. Motero anavala chiguduli m'chuuno mwao, ndi zingwe pamitu pao, nafika kwa mfumu ya Israele, nati, Kapolo wanu Benihadadi ati, Ndiloleni ndikhale ndi moyo. Nati iye, Akali moyo kodi? Ndiye mbale wanga. Tsono anthuwo anamyang'anitsa, nafulumira kugwira mauwo ngati anaterodi; nati, Mbale wanu Benihadadi ali moyo, Nati, Kamtengeni. Pamenepo Benihadadi anatuluka, nadza kwa iye, ndipo iye anamkweza m'galeta mwake. Ndipo Benihadadi anati kwa iye, Ndidzabweza midzi ija atate wanga analanda kwa atate wanu; ndipo mudzikonzere mabwalo a malonda m'Damasiko, monga umo atate wanga anadzikonzera m'Samariya. Ndi ine, ati Ahabu, ndikulola umuke ndi pangano ili. Tsono anapangana naye, namlola amuke. Ndipo wina wa ana a aneneri ananena ndi mnzake mwa mau a Yehova, Undikanthe ine. Koma munthuyo anakana kumkantha. Ndipo ananena naye, Popeza sunamvera mau a Yehova, taona, utalekana nane mkango udzakupha. Ndipo m'mene atalekana naye, mkango unampeza, numupha. Ndipo amene uja anakomana ndi munthu wina, nati, Undikanthe. Namkantha munthuyu, namtema pomkantha. Pamenepo mneneriyo anamuka, nadikira mfumu pamseu, nadzizimbaitsa ndi mpango pamaso pake. Ndipo popitapo mfumu, anafuula kwa mfumu, nati, Kapolo wanu analowa pakati pa nkhondo, ndipo taonani, munthu anapatuka nabwera ndi munthu kwa ine, nati, Tasunga munthu uyu; akasowa ndi chifukwa chilichonse moyo wako udzakhala m'malo mwa moyo wake, kapena udzalipa talente la siliva, Tsono pochita kapolo wanu apo ndi apo ndapeza palibe. Ndipo mfumu ya Israele inati kwa iye, Mlandu wako ukutsutsa momwemo, wadziweruza wekha. Ndipo iye anafulumira kuchotsa mpango kumaso kwake, ndi mfumu ya Israele inaona kuti anali mmodzi wa aneneri. Niti kwa iye, Atero Yehova, Popeza wataya m'dzanja lako munthu uja ndinati ndimuononge konse, moyo wako udzakhala m'malo mwa moyo wake, ndi anthu ako m'malo mwa anthu ake. Pamenepo mfumu ya Israele inanka kwao wamsunamo ndi wokwiya, nafika ku Samariya. Ndipo zitatha izi, kunaoneka zotere: Naboti wa ku Yezireele anali ndi munda wamphesa, unali m'Yezireelemo, m'mbali mwa nyumba ya Ahabu mfumu ya ku Samariya. Ndipo Ahabu analankhula ndi Naboti, nati, Ndipatse munda wako wamphesa ukhale munda wanga wa ndiwo, popeza uli pafupi ndi nyumba yanga; ndipo m'malo mwake ndidzakupatsa munda wamphesa wokoma woposa uwu; kapena kukakukomera ndidzakupatsa ndalama za pa mtengo wake. Ndipo Naboti anati kwa Ahabu, Pali Yehova, ndi pang'ono ponse ai, kuti ndikupatseni cholowa cha makolo anga. Ndipo Ahabu analowa m'nyumba mwake wamsunamo ndi wokwiya, chifukwa cha mau amene Naboti wa ku Yezireele adalankhula naye; popeza adati, Sindikupatsani cholowa cha makolo anga. M'mwemo anagona pa kama wake, nayang'ana kumbali, nakana kudya mkate. Koma Yezebele mkazi wake anadza kwa iye, nati kwa iye, Muchitiranji msunamo, kuti mukana kudya mkate? Nati kwa iye, Popeza ndinalankhula kwa Naboti wa ku Yezireele, ndinati kwa iye, Undigulitse munda wako ndi ndalama; kapena ukafuna, ndikupatsa munda wina m'malo mwake; koma anandiyankha, Sindikupatsani munda wanga wamphesa. Ndipo Yezebele mkazi wake anati kwa iye, Kodi mulamulira Aisraele tsopano ndinu? Taukani, idyani mkate, ukondwere mtima wanu; munda wa Naboti wa ku Yezireele ndidzakupatsani ndine. M'mwemo analemba akalata m'dzina la Ahabu nakhomerapo chizindikiro chake, natumiza akalatawo kwa akulu ndi omveka anali m'mudzi mwake, nakhala naye, Naboti. Ndipo analemba m'akalata, nati, Lalikirani kuti asale kudya, muike Naboti pooneka ndi anthu; ndipo muike anthu awiri, anthu oipa, pamaso pake, kuti amchitire umboni, ndi kuti, Watemberera Mulungu ndi mfumu; nimumtulutse ndi kumponya miyala kumupha. Ndipo anthu aja a mudzi wake, ndiwo akulu ndi omveka adakhala m'mudzi mwake, anachita monga Yezebele anawatumizira, monga munalembedwa m'akalata amene iye anawatumizira. Analalikira kuti asale kudya, naike Naboti pooneka ndi anthu. Ndipo anthu aja awiri oipawo analowa, nakhala pamaso pake, ndipo anthu oipawo anamchitira umboni wonama Nabotiyo, pamaso pa anthu onse, nati, Naboti anatemberera Mulungu ndi mfumu. Pamenepo anamtulutsa m'mudzi, namponya miyala, namupha. Pomwepo anatuma mau kwa Yezebele, nati, Naboti waponyedwa miyala, nafa. Ndipo kunali, atamva Yezebele kuti anamponya Naboti miyala nafa, Yezebele anati kwa Ahabu, Taukani, landirani munda wamphesa wa Naboti Myezireele uja anakana kukugulitsani ndi ndalama, popeza Naboti sali ndi moyo, koma wafa. Ndipo kunali, atamva Ahabu kuti Naboti Myezireele wafa, Ahabu anauka kukatsikira ku munda wamphesa wa Naboti, kuulandira. Ndipo mau a Yehova anadza kwa Eliya wa ku Tisibe, nati, Nyamuka, tsikira kukakomana ndi Ahabu mfumu ya Israele, akhala m'Samariya; taona, ali ku munda wamphesa wa Naboti kumene anatsikira kukaulandira. Ndipo uzilankhula naye, ndi kuti, Atero Yehova, Kodi wapha, nulandanso? Nulankhulenso naye, kuti, Atero Yehova, Paja agalu ananyambita mwazi wa Naboti pompaja agalu adzanyambita mwazi wako, inde wako. Ndipo Ahabu anati kwa Eliya, Wandipeza kodi, mdani wangawe? Nayankha, Ndakupeza; pokhala wadzigulitsa kuchita choipacho pamaso pa Yehova. Taona, ndidzakufikitsira choipa, ndi kuchotsa mbumba yako psiti; ndipo ndidzalikhira Ahabu mwana wamwamuna yense, ndi yense womangika ndi womasuka m'Israele; ndipo ndidzalinganiza nyumba yako ndi nyumba ya Yerobowamu mwana wa Nebati, ndi ya Baasa mwana wa Ahiya; chifukwa cha kuputa kumene unaputa nako mkwiyo wanga, ndi kuchimwitsa Israele. Ndipo za Yezebele yemwe Yehova ananena, nati, Agalu adzadya Yezebele ku linga la Yezireele. Mwana aliyense wa Ahabu amene adzafera m'mudzi, agalu adzamudya; ndipo iye amene adzafera kuthengo, mbalame za m'mlengalenga zidzamudya. Koma panalibe wina ngati Ahabu wakudzigulitsa kuchita choipa pamaso pa Yehova, amene Yezebele mkazi wake anamfulumiza. Ndipo anachita moipitsitsa kutsata mafano, monga mwa zonse amazichita Aamori, amene Yehova adawapirikitsa pamaso pa ana a Israele. Ndipo kunali, pakumva Ahabu mau amenewa, anang'amba zovala zake, navala chiguduli pathupi pake, nasala kudya, nagona pachiguduli, nayenda nyang'anyang'a. Pamenepo mau a Yehova anadza kwa Eliya wa ku Tisibe, nati, Waona umo wadzichepetsera Ahabu pamaso panga? Popeza adzichepetsa pamaso panga, sindidzafikitsa choipa chimenechi akali moyo iye; koma m'masiku a mwana wake ndidzachifikitsa pa nyumba yake. Ndipo Aaramu ndi Aisraele anakhala chete zaka zitatu, osathirana nkhondo. Koma kunachitika chaka chachitatu, kuti Yehosafati mfumu ya Yuda anatsikira kwa mfumu ya Israele. Ndipo mfumu ya Israele ananena ndi anyamata ake, nati, Kodi simudziwa kuti Ramoti Giliyadi ngwathu, ndipo tangokhala chete, osaulanditsa m'dzanja la mfumu ya Aramu. Tsono anati kwa Yehosafati, Kodi udzapita nane kunkhondo ku Ramoti Giliyadi? Ndipo Yehosafati anati kwa mfumu ya Israele, M'mene ukhalira iwe ndi momwe ndikhalira ndine; anthu anga monga anthu ako, akavalo anga monga akavalo ako. Ndipo Yehosafati ananena ndi mfumu ya Israele, Funsira ku mau a Yehova lero. Pamenepo mfumu ya Israele inasonkhanitsa aneneri ngati anthu mazana anai, nanena nao, Kodi ndizimuka kukathira nkhondo pa Ramoti Giliyadi, kapena ndileke? Nati iwo, Kweraniko; popeza Ambuye adzaupereka m'dzanja la mfumu. Koma Yehosafati anati, Kodi pano palibe mneneri wina wa Yehova, kuti tifunsire kwa iye? Ndipo mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Alipo munthu wina kuti tifunsire kwa Yehova mwa iye; koma ndimuda, popeza samanenera za ine zabwino, koma zoipa; ndiye Mikaya mwana wake wa Imila. Nati Yehosafati, Isamatero mfumu. Tsono mfumu ya Israele anaitana mdindo, nati, Kamtenge msanga Mikaya mwana wa Imila. Ndipo mfumu ya Israele ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakhala onse awiri, yense pa mpando wachifumu wake, ovala zovala zao zachifumu pabwalo popondera mphesa pa khomo la chipata cha Samariya; ndipo aneneri onse ananenera pamaso pao. Ndipo Zedekiya mwana wa Kenana anadzisulira nyanga zachitsulo, nati, Atero Yehova, Ndi izi mudzagunda nazo Aaramu mpaka atatha psiti. Ndipo aneneri onse ananena momwemo, nati, Kwerani ku Ramoti Giliyadi, ndipo mudzachita mwai; popeza Yehova adzaupereka m'dzanja la mfumu. Tsono mthenga uja udakaitana Mikaya unanena naye, nati, Taona, mau a aneneri avomerezana zokoma kwa mfumu ndi m'kamwa mmodzi; mau ako tsono afanane ndi mau a wina wa iwowo, nunene zabwino. Koma Mikaya anati, Pali Yehova, zimene Yehova adzanena nane ndidzanena ine. Ndipo atafika kwa mfumu, mfumu inati kwa iye, Mikaya, kodi tizimuka ku Ramoti Giliyadi kukathira nkhondo, kapena tileke? Nati iye, Kwerani, ndipo mudzachita mwai, popeza Yehova adzaupereka m'dzanja la mfumu. Ndipo mfumu inati, Ndikulumbiritse kangati kuti undiuze zoona zokhazokha m'dzina la Yehova? Nati iye, Ndinaona Aisraele onse obalalika pamapiri ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo Yehova anati, Izi zilibe mwini, yense abwerere ndi mtendere kunyumba yake. Pamenepo mfumu ya Israele inanena ndi Yehosafati, Kodi sindinakuuza kuti uyu sadzanenera za ine zabwino, koma zoipa? Ndipo anati, Chifukwa chake tamverani mau a Yehova, Ndinaona Yehova alikukhala pa mpando wake wachifumu, ndi khamu lonse lakumwamba lili chilili m'mbali mwake, ku dzanja lamanja ndi lamanzere. Nati Yehova, Adzanyenga Ahabu ndani, kuti akwere nagwe ku Ramoti Giliyadi? Ndipo anati wina mwakuti, wina mwakuti. Pamenepo mzimu wina unatuluka, nuima pamaso pa Yehova, nuti, Ndidzamnyenga ndine. Nati Yehova kwa iye, Motani? Nati, Ndidzatuluka, ndidzakhala mzimu wonama m'kamwa mwa aneneri ake onse. Nati, Udzamnyengadi, nudzakhozanso; tuluka, ukatero kumene. Ndipo tsopano taonani, Yehova waika mzimu wonama m'kamwa mwa aneneri anu onse awa, ndipo Yehova ananena choipa cha inu. Pamenepo Zedekiya mwana wa Kenana anasendera, napanda Mikaya patsaya, nati, Mzimu wa Yehova wandichokera bwanji, kulankhula ndi iwe? Mikaya nati, Taona, udzapenya tsiku lolowa iwe m'chipinda cha pakati kubisala. Pamenepo inati mfumu ya Israele, Tengani Mikaya, mumbweze kwa Amoni kalonga wa mudzi, ndi kwa Yowasi mwana wa mfumu; ndipo muziti, Itero mfumu, Khazikani uyu m'kaidi, mumdyetse chakudya cha nsautso, ndi madzi a nsautso, mpaka ndikabwera ndi mtendere. Ndipo Mikaya anati, Mukabwera ndithu ndi mtendere Yehova sanalankhule mwa ine. Nati, Mvetsani, anthu inu nonse. Tsono mfumu ya Israele ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakwera ku Ramoti Giliyadi. Ndipo mfumu ya Israele inanena ndi Yehosafati, Ine ndidzadzizimbaitsa, ndi kulowa kunkhondo, koma vala iwe zovala zako zachifumu. Ndipo mfumu ya Israele inadzizimbaitsa, nilowa kunkhondo. Tsono mfumu ya Aramu idalamulira akapitao makumi atatu mphambu ziwiri za magaleta ake, niti, Musaponyana ndi anthu ang'ono kapena akulu, koma ndi mfumu ya Israele yokha. Ndipo kunali, akapitao a magaleta ataona Yehosafati, anati, Zedi uyu ndiye mfumu ya Israele imene, napotolokera kukaponyana naye; koma Yehosafati anafuula. Ndipo pamene akapitao a magaleta anaona kuti sindiye mfumu ya Israele, anabwerera osampirikitsa. Ndipo munthu anakoka uta wake chiponyeponye, nalasa mfumu ya Israele pakati pa maluma a malaya achitsulo; tsono ananena ndi mnyamata wa galeta wake, Tembenuza dzanja lako, nundichotse kunkhondo, popeza ndalasidwa. Ndipo nkhondo inakula tsiku lomwelo, ndipo mfumu inagwirizidwa m'galeta mwake kupenyana ndi Aaramu, natsirizika madzulo; ndipo mwazi unatuluka m'bala pa phaka la galeta. Ndipo mfuu unafikira khamu lonse la nkhondo polowa dzuwa, ndi kuti, Yense kumudzi kwao, ndi yense ku dziko la kwao. Ndipo inafa mfumu, naifikitsa ku Samariya, naika mfumu m'Samariya. Ndipo potsuka galetayo pa thawale la ku Samariya agalu ananyambita mwazi wake, paja pamasamba akazi adama, monga mwa mau a Yehova amene ananenawo. Tsono machitidwe ena a Ahabu, ndi zonse adazichita, ndi nyumba ya minyanga adaimanga, ndi midzi yonse adaimanga, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele? Ndipo Ahabu anagona ndi makolo ake; ndi Ahaziya mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake. Koma Yehosafati mwana wa Asa anayamba kukhala mfumu ya Yuda chaka chachinai cha Ahabu mfumu ya Israele. Yehosafati anali wa zaka makumi atatu mphambu zisanu, pamene analowa ufumu, nakhala mfumu zaka makumi awiri mphambu zisanu m'Yerusalemu. Ndi dzina la amake linali Azuba mwana wa Sili. Ndipo anayenda m'njira yonse ya atate wake Asa, osapatukamo; nachita choyenera pamaso pa Yehova, koma misanje sanaichotse; anthu anapherabe nsembe, nafukiza zonunkhira pamsanje. Ndipo Yehosafati anachitana mtendere ndi mfumu ya Israele. Tsono machitidwe ena a Yehosafati, ndi mphamvu anaionetsayo, ndi umo anathira nkhondo, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda? Ndipo anachotsa m'dziko anyamata onyansa aja adatsalira masiku a atate wake Asa. Ndipo m'Edomu munalibe mfumu, koma kazembe wa mfumu. Yehosafati anamanga zombo za ku Tarisisi kukatenga golide ku Ofiri; koma sizinamuka, popeza zinaphwanyika pa Eziyoni-Gebere. Pamenepo Ahaziya mwana wa Ahabu ananena ndi Yehosafati, Anyamata anga amuke pamodzi ndi anyamata anu m'zombo. Koma Yehosafati anakana. Ndipo Yehosafati anagona ndi makolo ake, naikidwa ndi makolo ake m'mudzi wa Davide kholo lake; ndipo Yehoramu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake. Ahaziya mwana wa Ahabu anayamba kukhala mfumu ya Israele pa Samariya m'chaka chakhumi mphambu zisanu ndi ziwiri cha Yehosafati mfumu ya Yuda; nakhala mfumu ya Israele zaka ziwiri. Nachita choipa pamaso pa Yehova, nayenda m'njira ya atate wake, ndi ya amake, ndi ya Yerobowamu mwana wa Nebati, amene adachimwitsa Israele. Natumikira Baala, namweramira, naputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israele, monga umo anachitira atate wake. Ndipo atamwalira Ahabu, Mowabu anapandukana ndi Israele. Ndipo Ahaziya anagwa kuchokera pamwamba pa chipinda chake chosanja chinali ku Samariya, nadwala, natuma mithenga, nanena nayo, Mufunsire kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni ngati ndidzachira nthenda iyi. Koma mthenga wa Yehova anati kwa Eliya wa ku Tisibe, Nyamuka, kwera kukomana ndi mithenga ya mfumu ya Samariya, nunene nayo, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele, kuti mukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni? Chifukwa chake atero Yehova, Sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu. Nachoka Eliya. Ndipo mithenga inabwerera kwa iye, nanena nayo, Mwabwerera chifukwa ninji? Ndipo inanena naye, Munthu anakwera kukomana nafe, nati kwa ife, Kabwerereni kwa mfumu imene inakutumani inu, nimunene nayo, Atero Yehova, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele, kuti ulikutuma kukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni? Chifukwa chake sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu. Ndipo iye ananena nayo, Nanga maonekedwe ake a munthu anakwerayo kukomana nanu, nanena nanu mau awa, ndi otani? Ninena naye, Ndiye munthu wovala zaubweya, namangira m'chuuno mwake ndi lamba lachikopa. Nati iye, Ndiye Eliya wa ku Tisibe. Pamenepo mfumu inatuma kwa iye asilikali makumi asanu ndi mtsogoleri wao. Iye nakwera kunka kwa Eliya; ndipo taonani, analikukhala pamwamba pa phiri. Ndipo analankhula naye, Munthu wa Mulungu iwe, mfumu ikuti, Tsika. Nayankha Eliya, nanena ndi mtsogoleriyo, Ndikakhala ine munthu wa Mulungu, utsike moto wakumwamba, nunyeketse iwe ndi makumi asanu ako. Pamenepo unatsika moto kumwamba, nunyeketsa iye ndi makumi asanu ake. Ndipo anabwereza kutuma kwa iye mtsogoleri wina ndi makumi asanu ake. Ndipo iye anayankha nanena naye, Munthu wa Mulungu iwe, itero mfumu, Tsika msanga. Nayankha Eliya, nanena nao, Ndikakhala ine munthu wa Mulungu, utsike moto wakumwamba, nunyeketse iwe ndi makumi asanu ako. Pamenepo moto wa Mulungu unatsika kumwamba nunyeketsa iye ndi makumi asanu ake. Ndipo anabwerezanso kutuma mtsogoleri wachitatu ndi makumi asanu ake. Nakwera mtsogoleri wachitatuyo, nadzagwada ndi maondo ake pamaso pa Eliya, nampembedza, nanena naye, Munthu wa Mulungu inu, ndikupemphani, moyo wanga ndi moyo wa anyamata anu makumi asanu awa akhale a mtengo wake pamaso panu. Taonani, watsika moto wakumwamba, nunyeketsa atsogoleri awiri oyamba aja pamodzi ndi makumi asanu ao; koma tsopano moyo wanga ukhale wa mtengo wake pamaso panu. Pamenepo mthenga wa Yehova anati kwa Eliya, Tsika naye, usamuopa. Nanyamuka iye, natsikira naye kwa mfumu. Ndipo ananena nayo, Atero Yehova, Popeza watuma mithenga kukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni, kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele kufunsira mau ake? Chifukwa chake sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu. Motero anafa monga mwa mau a Yehova adanena Eliyawo. Ndipo Yehoramu analowa ufumu m'malo mwake chaka chachiwiri cha Yehoramu mwana wa Yehosafati mfumu ya Yuda, pakuti analibe mwana wamwamuna. Machitidwe ake ena tsono adawachita Ahaziya, sanalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele? Ndipo kunali, pamene Yehova adati akweze Eliya kumwamba ndi kamvulumvulu, Eliya anachokera ku Giligala pamodzi ndi Elisa. Ndipo Eliya anati kwa Elisa, Ukhale pompano pakuti Yehova wandituma ndinke ku Betele. Nati Elisa, Pali Mulungu, pali inu, sindikusiyani. Motero anatsikira iwo ku Betele. Ndipo ana a aneneri okhala ku Betele anatulukira Elisa, nanena naye, Kodi udziwa kuti Yehova akuchotsera lero mbuye wako, mtsogoleri wako? Nati, Inde ndidziwa, khalani muli chete. Ndipo Eliya anati kwa iye, Elisa, ukhale pompano, pakuti Yehova wandituma ku Yeriko. Nati iye, Pali Yehova, pali inu, sindikusiyani. Motero anadza ku Yeriko. Pamenepo ana a aneneri okhala ku Yeriko anayandikira kwa Elisa, nanena naye, Kodi udziwa kuti Yehova akuchotsera lero mbuye wako, mtsogoleri wako? Nati iye, Inde ndidziwa, khalani muli chete. Ndipo Eliya ananena naye, Ukhale pompano, pakuti Yehova wandituma ku Yordani. Nati iye, Pali Mulungu, pali inu, sindikusiyani. Napitirira iwo awiri. Ndipo anthu makumi asanu a ana a aneneri anapita, naima patali pandunji pao, iwo awiri naima ku Yordani. Ndipo Eliya anagwira chofunda chake, nachipindapinda napanda madzi, nagawikana kwina ndi kwina; ndipo anaoloka iwo onse awiri pansi pouma. Ndipo kunali ataoloka, Eliya anati kwa Elisa, Tapempha chimene ndikuchitire ndisanachotsedwe kwa iwe. Ndipo Elisa anati, Mundipatse magawo awiri a mzimu wanu akhale pa ine. Nati iye, Wapempha chinthu chapatali, koma ukandipenya pamene ndichotsedwa kwa iwe, kudzatero nawe; koma ukapanda kundipenyapo, sikudzatero ai. Ndipo kunachitika, akali chiyendere ndi kukambirana, taonani, anaoneka galeta wamoto ndi akavalo amoto, nawalekanitsa awiriwa; Eliya nakwera kumwamba ndi kamvulumvulu. Ndipo Elisa anapenya, nafuula, Atate wanga, atate wanga, galeta wa Israele ndi apakavalo ake! Koma analibe kumpenyanso; nagwira zovala zakezake, nazing'amba pakati. Pamenepo anatola chofunda chake cha Eliya chidamtayikiracho, nabwerera, naima m'mphepete mwa Yordani. Ndipo anatenga chofunda cha Eliya chidamtayikiracho, napanda madziwo, nati, Ali kuti Yehova Mulungu wa Eliya? Ndipo atapanda madziwo anagawikana kwina ndi kwina, naoloka Elisa. Ndipo pamene anampenya ana a aneneri okhala ku Yeriko pandunji pake, anati, Mzimu wa Eliya watera pa Elisa. Ndipo anadza kukomana naye, nadziweramitsa pansi kumaso kwake. Ndipo ananena naye, Taonani, tsono anyamata anufe tili nao amuna makumi asanu amphamvu, amuke kukafuna mbuye wanu; kapena wamkweza mzimu wa Yehova ndi kumponya pa phiri lina, kapena m'chigwa china. Koma anati, Musatumiza. Koma anamuumiriza kufikira anachita manyazi; pamenepo anati, Tumizani. Motero anatumiza amuna makumi asanu, namfunafuna iwo masiku atatu, osampeza. Nabwerera kwa iye ali chikhalire ku Yeriko, ndipo anati kwa iwo, Kodi sindinanena nanu, Musamuka? Ndipo amuna akumudzi anati kwa Elisa, Taonani, pamudzi pano mpabwino, monga umo aonera mbuye wanga; koma madzi ndi oipa, ndi nthaka siibalitsa. Pamenepo anati, Nditengereni chotengera chatsopano, muikemo mchere. Ndipo anabwera nacho kwa iye. Ndipo anatuluka kunka ku magwero a madzi, nathiramo mchere, nati, Atero Yehova, Ndachiritsa madzi awa, sikudzafumirakonso imfa, kapena kusabalitsa. Chotero madzi anachiritsidwa mpaka lero lino, monga mwa mau a Elisa ananenawo. Ndipo anachokako kukwera ku Betele, ndipo iye ali chikwerere m'njiramo, munatuluka anyamata ang'ono m'mudzimo, namseka, nati kwa iye, Takwera wadazi, takwera wadazi! Ndipo anacheuka, nawaona, nawatemberera m'dzina la Yehova. Ndipo kuthengo kunatuluka zimbalangondo ziwiri zazikazi, ndi kupwetedza mwa iwo ana makumi anai mphambu awiri. Ndipo anachokako kunka kuphiri la Karimele; nabwera kumeneko nafika ku Samariya. Ndipo Yehoramu mwana wa Ahabu analowa ufumu wa Israele m'Samariya m'chaka chakhumi mphambu zisanu ndi zitatu cha Yehosafati mfumu ya Yuda, nakhala mfumu zaka khumi ndi ziwiri. Nachita choipa pamaso pa Yehova, koma osati monga atate wake ndi amake; pakuti anachotsa choimiritsa cha Baala adachipanga atate wake. Koma anakangamira zoipa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene anachimwitsa nazo Israele, osalekana nazo. Ndipo Mesa mfumu ya Mowabu anali mwini nkhosa, akapereka kwa mfumu ya Israele ubweya wa anaankhosa zikwi zana limodzi, ndi wa mphongo zikwi zana limodzi. Koma kunachitika, atafa Ahabu mfumu ya Mowabu anapandukana ndi mfumu ya Israele. Ndipo mfumu Yehoramu anatuluka m'Samariya nthawi yomweyo, namemeza Aisraele onse. Nakatumiza mau kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, ndi kuti, Mfumu ya Mowabu wapandukana ndi ine; kodi udzamuka nane kukathira nkhondo pa Mowabu? Nati, Ndidzakwera: ine ndikhala ngati iwe, anthu anga ngati anthu ako, akavalo anga ngati akavalo ako. Ndipo anati, Tikwerere njira yiti? Nati iye, Njira ya ku chipululu cha Edomu. Namuka mfumu ya Israele, ndi mfumu ya Yuda, ndi mfumu ya Edomu, nazungulira njira ya masiku asanu ndi awiri; ndipo panalibe madzi kuti ankhondo amwe, kapena nyama zakuwatsata. Ndipo mfumu ya Israele inati, Kalanga ife! Pakuti Yehova waitana mafumu ife atatu kutipereka m'dzanja la Mowabu. Koma Yehosafati anati, Palibe pano mneneri wa Yehova kodi, kuti tifunsire Yehova mwa iye? Ndipo wina wa anyamata a mfumu ya Israele anayankha, nati, Elisa mwana wa Safati ali pano, ndiye uja anathira madzi m'manja a Eliya. Nati Yehosafati, Mau a Yehova ali ndi iyeyo. Pamenepo mfumu ya Israele, ndi Yehosafati, ndi mfumu ya Edomu, anatsikira kuli iye. Ndipo Elisa anati kwa mfumu ya Israele, Ndili ndi chiyani ndi inu? Mukani kwa aneneri a atate wanu, ndi kwa aneneri a amai wanu. Koma mfumu ya Israele inanena naye, Iai, pakuti Yehova anaitana mafumu ife atatu kutipereka m'dzanja la Mowabu. Ndipo Elisa anati, Pali Yehova wa makamu, amene ndiima pamaso pake, ndikadapanda kusamalira nkhope ya Yehosafati mfumu ya Yuda, sindikadakuyang'anitsani, kapena kukuonani. Koma tsopano, nditengereni wanthetemya. Ndipo kunali, wanthetemyayo ali chiimbire, dzanja la Yehova linamgwera. Ndipo anati, Atero Yehova, Kumbani m'chigwa muno mukhale maenje okhaokha. Pakuti atero Yehova, Simudzaona mphepo, kapena kuona mvula, koma chigwacho chidzadzala ndi madzi; ndipo mudzamwa inu, ndi ng'ombe zanu, ndi zoweta zanu. Ndipo ichi chidzapepuka pamaso pa Yehova; adzaperekanso Amowabu m'dzanja lanu. Ndipo mudzakantha midzi yonse ya malinga, ndi midzi yonse yosankhika, ndi kulikha mitengo yonse yabwino, ndi kufotsera zitsime zonse zamadzi, ndi kuipitsa pa nthaka ponse pabwino ndi miyala. Ndipo kunachitika m'mawa, pomapereka nsembe yaufa, taonani, anafika madzi odzera ku Edomu; ndipo dziko linadzala ndi madzi. Atamva tsono Amowabu onse kuti adakwera mafumu aja kuthirana nao nkhondo, anamemeza onse akumanga lamba m'chuuno ndi okulapo, naima iwo m'malire. Ndipo pamene anauka mamawa dzuwa linawala pamadzipo, naona Amowabu madzi ali pandunji pao ali psu ngati mwazi; nati, Uja ndi mwazi, atha kuonongana mafumu aja, anakanthana wina ndi mnzake; ndipo tsopano, tiyeni Amowabu inu, tikafunkhe. Ndipo pamene anafika ku misasa ya Israele, Aisraele ananyamuka, nakantha Amowabu, nathawa iwo pamaso pao; ndipo analowa m'dziko ndi kukantha Amowabu. Napasula midzi, naponya yense mwala wake panthaka ponse pabwino, naidzaza, nafotsera zitsime zonse zamadzi, nagwetsa mitengo yonse yabwino, kufikira anasiya miyala yake m'Kiri-Haresefi mokha; koma oponya miyala anauzinga, naukantha. Ndipo ataona mfumu ya Mowabu kuti nkhondo idamlaka, anapita nao anthu mazana asanu ndi awiri akusolola lupanga, kupyola kufikira kwa mfumu ya Edomu, koma sanakhoze. Pamenepo anagwira mwana wake wamwamuna woyamba amene akadakhala mfumu m'malo mwake, nampereka nsembe yopsereza palinga. Ndipo anakwiyira Israele kwambiri; potero anamchokera, nabwerera ku dziko lao. Ndipo wina wa akazi a ana a aneneri anafuula kwa Elisa, ndi kuti, Mnyamata wanu, mwamuna wanga wafa; mudziwa kuti mnyamata wanu anaopa Yehova; ndipo wafika wamangawa kunditengera ana anga awiri akhale akapolo ake. Ndipo Elisa anati kwa iye, Ndikuchitire chiyani? Undiuze m'nyumba mwako muli chiyani? Nati, Mdzakazi wanu alibe kanthu m'nyumba, koma mtsuko wa mafuta. Pamenepo anati, Kabwereke zotengera kwina kwa anansi ako onse, zotengera zopanda kanthu, zisakhale pang'ono. Nulowe, nudzitsekere wekha ndi ana ako amuna ndi kutsanulira m'zotengera zonsezi, nuike padera zodzalazo. Pamenepo anamchokera, nadzitsekera yekha ndi ana ake amuna; iwo namtengera zotengerazo, iye namatsanulira. Ndipo kunali, zitadzala zotengera, anati kwa mwana wake, Nditengere chotengera china. Nanena naye, Palibe chotengera china. Ndipo mafuta analeka. Pamenepo anadza, namfotokozera munthu wa Mulungu. Nati iye, Kagulitse mafuta, ukabwezere mangawa ako, ndi zotsalapo zikusunge iwe ndi ana ako. Ndipo linafika tsiku lakuti Elisa anapitirira kunka ku Sunemu, kumeneko kunali mkazi womveka; ameneyo anamuumiriza adye mkate. Potero pomapitirako iyeyo, ankawapatukirako kukadya mkate. Ndipo mkaziyo anati kwa mwamuna wake, Taona, tsopano ndidziwa kuti munthu uyu wakupitira pathu pano chipitire ndiye munthu woyera wa Mulungu. Timmangire kachipinda kosanja, timuikirenso komweko kama, ndi gome, ndi mpando, ndi choikapo nyali; ndipo kudzatero kuti akatidzera alowe m'mwemo. Ndipo linadza tsiku lakuti anafikako, nalowa m'chipinda chosanja, nagona komweko. Nati kwa Gehazi mnyamata wake, Itana Msunamu uja. Namuitana, naima mkaziyo pamaso pake. Ndipo anati kwa iye, Ufunse mkaziyu tsopano, kuti, Taona watisungira ndi kusamalira uku konse; nanga tikuchitire iwe chiyani? Kodi tikunenere kwa mfumu, kapena kwa kazembe wa nkhondo? Koma anati, Ndikhala ine pakati pa anthu a mtundu wanga. Pamenepo anati, Nanga timchitire iye chiyani? Nati Gehazi, Zedi alibe mwana, ndi mwamuna wake wakalamba. Nati, Kamuitane. Namuitana, naima pakhomo mkaziyo. Ndipo anati, Nyengo yino chaka chikudzachi udzafukata mwana wamwamuna. Koma anati, Iai, mbuyanga, munthu wa Mulungu, musanamiza mdzakazi wanu. Ndipo mkaziyo anaima, naona mwana wamwamuna nyengo yomweyo chaka chimene chija Elisa adanena naye. Ndipo atakula mwanayo, linadza tsiku lakuti anatuluka kunka kwa atate wake, ali kwa omweta tirigu. Nati kwa atate wake, Mutu wanga, mutu wanga! Pamenepo anati kwa mnyamata, Umnyamule umuke naye kwa amake. Namnyamula, napita naye kwa amake. Ndipo anakhala pa maondo ake kufikira usana, namwalira. Ndipo anakwera, namgoneka pa kama wa munthu wa Mulungu, natuluka, namtsekera. Naitana mwamuna wake, nati, Nditumizire mmodzi wa anyamata ndi bulu mmodzi, kuti ndithamangire kwa munthu uja wa Mulungu, ndi kubweranso. Ndipo anati, Ulikumuka kwa iye lero chifukwa ninji? Ngati mwezi wakhala, kapena mpa Sabata? Koma anati, Kuli bwino. Pamenepo anamangirira bulu mbereko, nati kwa mnyamata wake, Kusa, tiye; usandilezetsa kuyendaku, ndikapanda kukuuza. Potero anamuka, nafika kwa munthu wa Mulungu kuphiri la Karimele. Ndipo kunali, pakumuona munthu wa Mulungu alinkudza kutali, anati kwa Gehazi mnyamata wake, Tapenya, suyo Msunamu uja; uthamange tsopano kukomana naye, nunene naye, Muli bwino kodi? Mwamuna wanu ali bwino? Mwanayo ali bwino? Ndipo anati, Ali bwino. Ndipo pofika kwa munthu wa Mulungu kuphiri anamgwira mapazi. Ndipo Gehazi anayandikira kuti amkankhe; koma munthu wa Mulungu anati, Umleke, pakuti mtima wake ulikumuwawa; ndipo Yehova wandibisira osandiuza ichi. Ndipo mkaziyo anati, Ngati ndinapempha mwana kwa mbuyanga? Kodi sindinati, Musandinyenga? Pamenepo anati kwa Gehazi, Udzimangire m'chuuno, nutenge ndodo yanga m'dzanja lako, numuke; ukakomana ndi munthu usampatse moni; wina akakupatsa moni usamyankhe; ukaike ndodo yanga pankhope pa mwanayo. Koma make wa mwana anati, Pali Yehova, pali inunso, ngati nkukusiyani. Ndipo ananyamuka, namtsata. Nawatsogolera Gehazi, naika ndodo pankhope pa mwanayo; koma mwanayo analibe mau, kapena kusamalira. Motero anabwerera kukomana naye, namuuza kuti, Sanauke mwanayo. Ndipo pamene Elisa analowa m'nyumba, taonani, mwanayo ngwakufa, adamgoneka pakama pake. Nalowa Elisa, nadzitsekera awiriwa, napemphera kwa Yehova. Nakwera, nagona pa mwanayo ndi kulinganiza pakamwa pake ndi pakamwa pake, maso ake ndi maso ake, zikhato zake ndi zikhato zake, nadzitambasula pa iye, ndi mnofu wa mwana unafunda. Pamenepo anabwera nayenda m'nyumba, chakuno kamodzi, chauko kamodzi; nakwera, nadzitambasuliranso pa iye; ndi mwana anayetsemula kasanu ndi kawiri, natsegula mwanayo maso ake. Pamenepo anaitana Gehazi, nati, Kaitane Msunamu uja. Namuitana. Ndipo atalowa kuli iye, anati, Nyamula mwana wako. Iye nalowa, nagwa pa mapazi ake, nadziweramitsa pansi; nanyamula mwana wake, natuluka. Ndipo Elisa anabwera ku Giligala, koma m'dzikomo munali njala; ndi ana a aneneri anali kukhala pansi pamaso pake; ndipo anati kwa mnyamata wake, Ika nkhali yaikuluyo, uphikire ana a aneneri. Natuluka wina kukatchera ndiwo kuthengo, napeza chonga ngati mpesa, natcherapo zipuzi kudzaza m'funga mwake, nadza, nazichekerachekera m'nkhali ya chakudya, popeza sanazidziwe. Pamenepo anagawira anthu kuti adye. Koma kunali, pakudya chakudyacho, anafuula nati, Munthu wa Mulungu, muli imfa m'nkhalimo. Ndipo sanathe kudyako. Pamenepo anati, Bwera naoni ufa. Nathira m'nkhalimo; nati, Gawirani anthu kuti adye. Ndipo m'nkhalimo munalibe chowawa. Ndipo anadza munthu kuchokera ku Baala-Salisa, nabwera nayo m'thumba mikate ya zipatso zoyamba kwa munthu wa Mulungu, mikate ya barele makumi awiri, ndi ngala zaziwisi za tirigu zosaomba. Ndipo anati, Uwapatse anthu kuti adye. Koma mnyamata wake anati, Chiyani? Ndigawire amuna zana ichi kodi? Koma anati, Uwapatse anthu kuti adye; pakuti atero Yehova, Adzadya nadzasiyako. Potero anawagawira, nadya, nasiyapo, monga mwa mau a Yehova. Ndipo Naamani kazembe wa khamu la nkhondo la mfumu ya Aramu anali munthu womveka pamaso pa mbuyake, ndi waulemu; popeza mwa iye Yehova adapulumutsa Aaramu; ndiyenso ngwazi, koma wakhate. Ndipo Aaramu adatuluka magulumagulu, nabwera nalo m'ndende buthu lochokera ku dziko la Israele, natumikira mkazi wa Naamani iyeyu. Nati uyu kwa mbuyake wamkazi, Mbuye wanga akadakhala kwa mneneri ali m'Samariya, akadamchiritsa khate lake. Ndipo analowa wina, nauza mbuye wake, kuti, Buthulo lofuma ku dziko la Israele lanena zakutizakuti. Pamenepo mfumu ya Aramu inati, Tiye, muka, ndidzatumiza kalata kwa mfumu ya Israele. Pamenepo anachoka, atatenga siliva matalente khumi, ndi golide masekeli zikwi zisanu ndi chimodzi, ndi zovala zakusintha khumi. Ndipo anafika kwa mfumu ya Israele ndi kalata, wakuti, Pakulandira kalata uyu, taonani, ndatumiza Naamani mnyamata wanga kwa inu, kuti mumchiritse khate lake. Ndipo kunali atawerenga kalatayu mfumu ya Israele, anang'amba zovala zake, nati, Ngati ndine Mulungu, kupha ndi kubwezera moyo, kuti ameneyo atumiza kwa ine kumchiritsa munthu khate lake? Pakuti dziwani, nimupenye, kuti alikufuna chifukwa pa ine. Koma kunali, pamene Elisa munthu wa Mulungu anamva kuti mfumu ya Israele adang'amba zovala zake, anatumiza mau kwa mfumu, ndi kuti, Mwang'amba zovala zanu chifukwa ninji? Adzetu kwa ine, ndipo adzadziwa kuti muli mneneri m'Israele. M'mwemo Naamani anadza ndi akavalo ake ndi magaleta ake, naima pakhomo pa nyumba ya Elisa. Ndipo Elisa anamtumira mthenga, ndi kuti, Kasambe m'Yordani kasanu ndi kawiri, ndi mnofu wako udzabwerera momwe, nudzakhala wokonzeka. Koma Naamani adapsa mtima, nachoka, nati, Taona, ndinati m'mtima mwanga, kutuluka adzanditulukira, nadzaima ndi kuitana pa dzina la Yehova Mulungu wake, ndi kuweyula dzanja lake pamalopo, ndi kuchiritsa wakhateyo. Nanga Abana ndi Faripara, mitsinje ya Damasiko, siiposa kodi madzi onse a m'Israele? Ndilekerenji kukasamba m'mwemo, ndi kukonzeka? Natembenuka, nachoka molunda. Pamenepo anyamata ake anasendera, nanena naye, nati, Atate wanga, mneneri akadakuuzani chinthu chachikulu, simukadachichita kodi? Koposa kotani nanga ponena iye, Samba, nukonzeke? Potero anatsika, namira m'Yordani kasanu ndi kawiri, monga adanena munthu wa Mulunguyo; ndi mnofu wake unabwera monga mnofu wa mwana wamng'ono, nakonzeka. Pamenepo anabwerera kwa munthu wa Mulungu iye ndi gulu lake lonse, nadzaima pamaso pake, nati, Taonani, tsopano ndidziwa kuti palibe Mulungu pa dziko lonse lapansi, koma kwa Israele ndiko; ndipo tsopano, mulandire chakukuyamikani nacho kwa mnyamata wanu. Koma anati, Pali Yehova, amene ndiima pamaso pake, sindidzalandira kanthu. Ndipo anamkakamiza achilandire, koma anakana. Ndipo Naamani anati, Mukakana, andipatse akatundu a dothi osenza nyuru ziwiri; pakuti mnyamata wanu sadzaperekanso nsembe yopsereza kapena yophera kwa milungu ina, koma kwa Yehova. Yehova akhululukire mnyamata wanu mwa ichi; akalowa mbuye wanga m'nyumba ya Rimoni kulambiramo, nakatsamira pa dzanja langa, nanenso ndikagwadira m'nyumba ya Rimoni, pakugwadira ine m'nyumba ya Rimoni, Yehova akhululukire mnyamata wanu mwa ichi. Ndipo ananena naye, Pita mumtendere. Ndipo anachoka, nayenda kanthawi. Koma Gehazi, mnyamata wa Elisa, munthu wa Mulungu, anati, Taona, mbuye wanga analekera Naamani uyu wa ku Aramu osalandira m'manja ake chimene anabwera nacho; pali Yehova, ndidzathamangira ndi kulandira kanthu kwa iye. Motero Gehazi anatsata Naamani. Ndipo pamene Naamani anaona wina alikumthamangira, anatsika pagaleta kukomana naye, nati, Nkwabwino kodi? Nati, Kuli bwino. Mbuye wanga wandituma, ndi kuti, Taonani, andifikira tsopano apa anyamata awiri a ana a aneneri, ochokera ku mapiri a Efuremu; muwapatse talente wa siliva, ndi zovala zosintha ziwiri. Nati Naamani, Ulole ulandire matalente awiri. Namkakamiza namanga matalente awiri a siliva m'matumba awiri, ndi zovala zosintha ziwiri, nasenzetsa anyamata ake awiri; iwo anatsogola atazisenza. Ndipo pamene anafika kumsanje anazilandira m'manja mwao, naziika m'nyumba; nauza anthuwo amuke, iwo nachoka. Pamenepo analowa, naima kwa mbuye wake. Ndipo Elisa ananena naye, Ufuma kuti Gehazi? Nati, Ngati mnyamata wanu wayenda konse? Ndipo anati kwa iye, Mtima wanga sunakuperekeza kodi, umo munthuyo anatembenuka pa galeta wake kukomana ndi iwe? Kodi nyengo yino ndiyo yakulandira siliva, ndi kulandira zovala, ndi minda ya azitona, ndi yampesa, ndi nkhosa, ndi ng'ombe, ndi akapolo, ndi adzakazi? Chifukwa chake khate la Naamani lidzakumamatira iwe ndi mbumba yako chikhalire. Ndipo anatuluka pamaso pake wakhate wa mbu ngati chipale chofewa. Ndipo ana a aneneri anati kwa Elisa, Taonani tsono, pamalo tikhalapo ife pamaso panu patichepera Mutilole tipite ku Yordani, tikatengeko aliyense mtengo, tidzimangire malo komweko, tikhalepo. Nati, Mukani. Ndipo wina anati, Mulole mupite nafe anyamata anu. Nati, Ndidzamuka. Namuka nao, nafika ku Yordani, iwo natema mitengo. Ndipo wina analinkudula mtengo nkhwangwa inagwa m'madzi; ndipo anafuula, nati, Kalanga ine mbuyanga! Popeza njobwereka. Nati munthu wa Mulungu, Yagwera pati? Namuonetsapo yagwera. Pamenepo anadula kamtengo, nakaponya pomwepo, nayandamitsa nkhwangwayo. Nati, Katole. Natambasula dzanja lake, naitenga. Ndipo mfumu ya Aramu inalinkuchita nkhondo ndi Israele, nipangana ndi anyamata ake, kuti, Misasa yanga idzakhala pakutipakuti. Ndipo munthu wa Mulunguyo anatuma mau kwa mfumu ya Israele, ndi kuti, Muchenjere musapite pakuti, popeza Aaramu alikutsikira uko. Pamenepo mfumu ya Israele inatumiza kumene munthu wa Mulungu anamuuzako ndi kumchenjeza; nadzisunga osapitako, kawirikawiri. Koma mtima wa mfumu ya Aramu unavutika kwambiri pa ichicho, naitana anyamata ake, nanena nao, Kodi simudzandiuza wina wa ife wovomerezana ndi mfumu ya Israele ndani? Nati mmodzi wa anyamata ake, Iai, mbuye wanga mfumu; koma Elisa, mneneriyo ali ku Israele ndiye amafotokozera mfumu ya Israele mau muwanena m'kati mwake mwa chipinda chanu chogonamo. Nati iye, Kamuoneni komwe ali; ndikatume munthu kumtenga. Ndipo anamuuza kuti, Ali ku Dotani. Pamenepo anatumizako akavalo ndi magaleta ndi khamu lalikulu, nafikako usiku, nauzinga mudziwo. Ndipo atalawirira mamawa mnyamata wa munthu wa Mulungu, natuluka, taonani, khamu la nkhondo linazinga mudzi ndi akavalo ndi magaleta. Ndi mnyamata wake ananena naye, Kalanga ine, mbuye wanga! Tichitenji? Nati iye, Usaopa, pakuti okhala pamodzi ndi ife achuluka koposa aja okhala pamodzi ndi iwo. Ndipo Elisa anapemphera, nati, Yehova, mumtsegulire maso ake kuti aone. Pamenepo Yehova anamtsegulira maso mnyamatayo, napenya iye, ndipo taonani, paphiripo panadzala ndi akavalo ndi magaleta amoto akumzinga Elisa. Ndipo atatsikira pali iye, Elisa anapemphera kwa Yehova, nati, Mukanthe mtundu uwu uchite khungu. Ndipo Iye anawakantha, nawachititsa khungu, monga mwa mau a Elisa. Ndipo Elisa ananena nao, Ngati njira ndi iyi? Ngati mudzi ndi uwu? Munditsate ine, ndidzakufikitsani kwa munthu mumfunayo; nawatsogolera ku Samariya. Ndipo kunali, pakufika ku Samariya, Elisa anati, Yehova, muwakanganulire awa maso kuti aone. Nawakanganulira Yehova maso ao, naona iwo, ndipo tapenyani, ali pakati pa Samariya. Niti mfumu ya Israele kwa Elisa pakuwaona, Atate wanga, ndiwakanthe kodi, ndiwakanthe? Nati, Musawakanthe; kodi mumakantha omwe mwawagwira ndi lupanga ndi uta wanu? Apatseni mkate ndi madzi adye namwe, namuke kwa mbuye wao. Ndipo anawakonzera chakudya chambiri, nadya namwa iwo; nawauza amuke; namuka kwa mbuye wao. Ndipo magulu a Aramu sanadzenso ku dziko la Israele. Ndipo zitatha izi, Benihadadi mfumu ya Aramu anamemeza khamu lake lonse, nakwera, namangira misasa Samariya. Koma m'Samariya munali njala yaikulu; ndipo taonani, anaumangira misasa mpaka mutu wa bulu unagulidwa masekeli a siliva makumi asanu ndi atatu; ndi limodzi la magawo anai la muyeso wa kabu wa zitosi za nkhunda linagulidwa ndi masekeli asiliva asanu. Ndipo popita mfumu ya Israele alikuyenda palinga, mkazi anamfuulira, nati, Ndithandizeni, mbuye wanga mfumu. Nati iye, Akapanda kukuthandiza Yehova, ndikaona kuti kokuthandiza ine? Kudwale kodi, kapena popondera mphesa? Nanena naye mfumu, Ufunanji? Nati iye, Mnzanga uyu ananena ndi ine, Tenga mwana wako timudye lero, ndi mwana wanga timudye mawa. Ndipo tinaphika mwana wanga ndi kumudya, ndi mawa wake ndinanena naye, Tenga mwana wako, timudye; koma wambisa mwana wake. Ndipo pakumva mfumu mau a mkaziyo, anang'amba zovala zake alinkupita nayenda palinga, anthu napenya; ndipo taonani, pali chiguduli m'kati pa thupi lake. Nati iye, Andilange Mulungu naonjezeko, ngati mutu wa Elisa mwana wa Safati uti ukhale pa iye lero lino. Koma Elisa anakhala pansi m'nyumba mwake, ndi akulu anakhala pansi pamodzi naye; ndipo mfumu inatuma munthu amtsogolere, koma asanafike kwa Elisa mthengayo, anati kwa akulu, Mwapenya kodi m'mene mwana uyu wambanda watumiza munthu kuchotsa mutu wanga? Taonani, pakufika mthengayo mutseke pakhomo, mumkankhe ndi chitseko. Kodi mapazi a mbuye wake samveka dididi pambuyo pake? Akali chilankhulire nao, tapenyani, wamtsikira mthengayo; ndi mfumu inati, Taonani, choipa ichi chichokera kwa Yehova; ndilindiranjinso Yehova? Ndipo Elisa anati, Mverani mau a Yehova; atero Yehova, Mawa dzuwa lino adzagula muyeso wa ufa ndi sekeli, adzagulanso miyeso iwiri ya barele ndi sekeli, pa chipata cha Samariya. Pamenepo kazembe amene mfumu ankatsamira pa dzanja lake anamyankha munthu wa Mulungu, nati, Taonani, Yehova angachite mazenera m'mwamba chidzachitika ichi kodi? Nati iye, Taona, udzachiona ndi maso ako, koma iwe sudzadyako ai. Koma polowera pa chipata panali amuna anai akhate, nanenana wina ndi mnzake, Tikhaliranji kuno mpaka kufa? Tikati, Tilowe m'mudzi, m'mudzi muli njala, tidzafa m'mwemo; tikakhala pompano, tidzafanso. Tiyeni tsono, tigwe ku misasa ya Aaramu; akatisunga ndi moyo, tidzakhala ndi moyo; akatipha, tangokufa. Nanyamuka iwo kuli sisiro kukalowa ku misasa ya Aaramu; koma pofika polekezera pake pa misasa ya Aaramu, taonani, panalibe munthu pomwepo. Popeza Yehova adamvetsa khamu la Aaramu phokoso la magaleta ndi mkokomo wa akavalo, phokoso la nkhondo yaikulu; nanenana wina ndi mnzake, Taonani mfumu ya Israele watimemezera mafumu a Ahiti ndi mafumu a Aejipito, atigwere. Nanyamuka, nathawa kuli sisiro, nasiya mahema ao, ndi akavalo ao, ndi abulu ao, misasa ili chimangire; nathawa apulumutse moyo wao. Ndipo pofika akhate ao polekezera pa misasa, analowa m'hema mmodzi, nadya namwa, natengako siliva ndi golide ndi zovala, namuka, nazibisa; nabwerera, nalowa m'hema mwina, natengako, namuka, nazibisa. Pamenepo ananenana wina ndi mnzake, Sitilikuchita bwino ife; tsiku lino ndilo tsiku la uthenga wabwino, ndipo tilikukhala chete; tikachedwa kufikira kwacha, mphulupulu yathu idzatipeza; tiyeni tsono, timuke, tifotokozere a m'nyumba ya mfumu. Nadza iwo, naitana mlonda wa mudzi, namfotokozera; ndi kuti, Tinafika ku misasa ya Aaramu, ndipo taonani, palibe munthu pomwepo, kapena mau a munthu, koma akavalo omanga, ndi abulu omanga, ndi mahema ali chimangire. Ndipo iye anaitana alonda ena, ndi iwo anafotokozera a m'nyumba ya mfumu. Niuka mfumu usiku, ninena ndi anyamata ake, Ndikufotokozereni m'mene Aaramu atichitira ife. Adziwa kuti tagwidwa ndi njala, natuluka m'misasa, nabisala kuthengo, ndi kuti, Pamene atuluka m'mudzi tidzawagwira ndi moyo ndi kulowa m'mudzimo. Nayankha mmodzi wa anyamata ake, nati, Atenge tsono akavalo otsala asanu, ndiwo otsala m'mudzi; taonani, adzanga unyinji wonse wa Israele otsalawo, kapena adzanga unyinji wonse wa Israele otsirizika; tiwatumize tione. Motero anatenga magaleta awiri ndi akavalo ao; ndipo mfumu inawatumiza alondole khamu la Aaramu, ndi kuti, Mukani mukaone. Ndipo anawalondola mpaka ku Yordani; ndipo taonani, m'njira monse munadzala ndi zovala ndi akatundu adazitaya Aaramu m'kufulumira kwao. Nibwera mithenga, nifotokozera mfumu. Natuluka anthu, nafunkha m'misasa ya Aaramu. Ndipo anagula miyeso ya ufa ndi sekeli, nagulanso miyeso iwiri ya barele ndi sekeli, monga umo adanenera Yehova. Koma mfumu idayang'anitsa pachipata kazembe amene uja idafotsamira pa dzanja lake; ndipo anthu anampondereza pachipata, nafa iye, monga umo adanenera munthu wa Mulungu, ponena paja anamtsikira mfumu. Ndipo kunachitika, monga adanena munthu wa Mulungu kwa mfumu, ndi kuti, Adzagula miyeso iwiri ya barele ndi sekeli, adzagulanso muyeso wa ufa ndi sekeli; kudzatero mawa, dzuwa lino, pa chipata cha Samariya; ndipo kazembe uja adayankha munthu wa Mulunguyo, nati, Taonani tsono, Yehova angachite mazenera m'mwamba, chikachitika ichi kodi? Nati iye, Taona, udzachiona ichi ndi maso ako, koma osadyako ai; kudamchitikira momwemo; popeza anthu anampondereza pachipata nafa iye. Ndipo Elisa ananena ndi mkazi uja adamuukitsira mwana wake, kuti, Nyamuka, numuke iwe ndi banja lako, nugonere komwe ukaone malo; pakuti Yehova waitana njala, nidzagwera dziko zaka zisanu ndi ziwiri. Nanyamuka mkaziyo, nachita monga mwa mau a munthu wa Mulunguyo, namuka ndi banja lake, nagonera m'dziko la Afilisti zaka zisanu ndi ziwiri. Ndipo pakutha pake pa zaka zisanu ndi ziwirizo, mkaziyo anabwera kuchoka m'dziko la Afilisti, natuluka kukanena za nyumba yake ndi munda wake kwa mfumu. Koma mfumu inalikulankhula ndi Gehazi mnyamata wa munthu wa Mulungu, ndi kuti, Ndifotokozere zazikulu zonse Elisa wazichita. Ndipo kunali, alimkufotokozera mfumu m'mene adamuukitsira wakufayo, taonani, mkaziyo adamuukitsira mwana wake ananena za nyumba yake ndi munda wake kwa mfumu. Nati Gehazi, Mbuye wanga mfumu, suyu mkaziyo, suyu mwana wake Elisa anamuukitsayo? Ndipo pofunsa mfumu, mkaziyo anaisimbira. Pamenepo mfumu anamuikira mdindo, ndi kuti, Bwezetsa zake zonse ndi zipatso zonse za m'munda, chichokere iye m'dziko mpaka lero lino. Ndipo Elisa anafika ku Damasiko, podwala Benihadadi mfumu ya Aramu; ndipo anamuuza, kuti, Munthu wa Mulungu wadza kuno. Niti mfumu kwa Hazaele, Tenga chaufulu m'dzanja lako, nukakumane naye munthu wa Mulungu, nukafunsire Yehova mwa iye, ndi kuti, Ndidzachira kodi nthenda iyi? Namuka Hazaele kukakomana naye, napita nacho chaufulu, ndicho cha zokoma zonse za m'Damasiko, zosenza ngamira makumi anai, nafika naima pamaso pake, nati, Mwana wanu Benihadadi mfumu ya Aramu, wandituma ine kwa inu, ndi kuti, Kodi ndidzachira nthenda iyi? Nanena naye Elisa, Kamuuze, kuti, Sudzachira konse; popeza Yehova wandionetsa kuti adzafa ndithu. Ndipo anamyang'ana chidwi, mpaka anachita manyazi, nalira misozi munthu wa Mulungu. Nati Hazaele, Muliriranji, mbuye wanga? Nayankha iye, Popeza ndidziwa choipa udzachitira ana a Israele; udzatentha malinga ao ndi moto, nudzapha anyamata ao ndi lupanga, nudzaphwanya makanda ao, nudzang'amba akazi ao okhala ndi pakati. Nati Hazaele, Koma nanga kapolo wanu ali chiyani, ndiye galu, kuti akachite chinthu chachikulu ichi? Nayankha Elisa, Yehova wandionetsa kuti udzakhala mfumu ya pa Aramu. Ndipo anachoka kwa Elisa, nadza kwa mbuye wake; ameneyo ananena naye, Anakuuza chiyani Elisa? Nati iye, Anandiuza kuti mudzachira ndithu. Ndipo kunali m'mawa mwake, anatenga chimbwi, nachiviika m'madzi, nachiphimba pankhope pa mfumu, nifa; ndipo Hazaele analowa ufumu m'malo mwake. Ndipo chaka chachisanu cha Yoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Israele, pokhala Yehosafati mfumu ya Yuda, Yehoramu mwana wa Yehosafati analowa ufumu. Ndiye wa zaka makumi atatu ndi chiwiri polowa ufumu wake, nachita ufumu zaka zisanu ndi zitatu ku Yerusalemu. Nayenda m'njira ya mafumu a Israele, m'mene inachitira nyumba ya Ahabu; pakuti mkazi wake ndiye mwana wa Ahabu, nachita iye choipa pamaso pa Yehova. Koma Yehova sanafune kuononga Yuda, chifukwa cha Davide mtumiki wake monga adamuuza, kuti adzampatsa nyali ya kwa ana ake kosalekeza. Masiku ake Aedomu anapanduka ku ulamuliro wa Yuda, nadziikira mfumu okha. Pamenepo Yoramu anaoloka kunka ku Zairi, ndi magaleta ake onse pamodzi naye; nauka iye usiku, nakantha Aedomu akumzinga ndi nduna za magaleta, nathawira anthu kwa mahema ao. Motero Aedomu anapanduka ku ulamuliro wa Yuda mpaka lero lino. Ndipo Alibina anapanduka nthawi yomweyi. Ndi machitidwe ena a Yoramu, ndi zonse anazichita, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda. Nagona Yoramu ndi makolo ake, naikidwa pamodzi ndi makolo ake m'mudzi wa Davide; ndipo Ahaziya mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake. Chaka chakhumi ndi ziwiri cha Yoramu mwana wa Ahabu mfumu Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda analowa ufumu wake. Ahaziya ndiye wa zaka makumi awiri mphambu ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu chaka chimodzi. Ndi dzina la make ndiye Ataliya mdzukulu wa Omuri mfumu ya Israele. Ndipo anayenda m'njira ya nyumba ya Ahabu, nachita choipa pamaso pa Yehova, m'mene inachitira nyumba ya Ahabu; pakuti ndiye wa chibale cha banja la Ahabu. Ndipo anamuka Yoramu mwana wa Ahabu kukathira nkhondo pa Hazaele mfumu ya Aramu ku Ramoti Giliyadi; ndi Aaramu analasa Yoramu. Ndipo mfumu Yoramu anabwera kuti ampoletse m'Yezireele mabalawo adamkantha Aaramu ku Rama, polimbana naye Hazaele mfumu ya Aramu. Natsikirako Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda kukamuona Yoramu mwana wa Ahabu m'Yezireele, pakuti anadwala. Ndipo Elisa mneneriyo anaitana mmodzi wa ana a aneneri, nanena naye, Udzimangire m'chuuno, nutenge nsupa iyi ya mafuta m'dzanja mwako, numuke ku Ramoti Giliyadi. Ndipo ukafikako, ukaunguzeko Yehu mwana wa Yehosafati mwana wa Nimisi, nulowe numnyamukitse pakati pa abale ake, nupite naye ku chipinda cham'katimo. Nutenge nsupa ya mafutayo, nuwatsanulire pamutu pake, nunene, Atero Yehova, Ndakudzoza iwe ukhale mfumu pa Israele. Utatero, tsegula pakhomo, nuthawe osachedwa, Pamenepo mnyamatayo, ndiye mneneri, anamuka ku Ramoti Giliyadi. Nalowa, ndipo taonani, akazembe a khamu alikukhala pansi; nati iye, Ndili ndi mau kwa inu, kazembe. Nati Yehu, Kwa yani wa ife tonse? Nati iye, Kwa inu, kazembe. Nanyamuka, nalowa m'nyumba; ndipo anatsanulira mafutawo pamutu pake, nanena naye, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Ndakudzoza ukhale mfumu ya pa anthu a Yehova, ndiwo Aisraele. Nudzakantha nyumba ya Ahabu mbuye wako, kuti ndibwezere chilango cha mwazi wa atumiki anga aneneri, ndi mwazi wa atumiki onse a Yehova, dzanja la Yezebele. Popeza nyumba yonse ya Ahabu idzaonongeka, ndipo ndidzalikhira Ahabu ana amuna onse womangika ndi womasuka m'Israele. Ndipo ndidzalinganiza nyumba ya Ahabu ndi nyumba ya Yerobowamu mwana wa Nebati, ndi nyumba ya Baasa mwana wa Ahiya. Ndipo agalu adzamudya Yezebele pa dera la Yezireele, wopanda wina wakumuika. Pamenepo anatsegula pakhomo, nathawa. Ndipo Yehu anatulukira kwa anyamata a mbuye wake, nanena naye wina, Mtendere kodi? Anakudzera chifukwa ninji wamisala uyu? Nanena nao, Mumdziwa munthuyo ndi makambidwe ake. Nati iwo, Kunama uku; utifotokozere tsono. Nati iye, Anati kwa ine chakutichakuti; ndi kuti, Atero Yehova, Ndakudzoza mfumu pa Israele. Nafulumira iwo, nagwira yense chofunda chake, nachiyala pokhala iye pachiunda, naomba lipenga, nati, Yehu ndiye mfumu. Motero Yehu mwana wa Yehosafati mwana wa Nimisi anapandukira Yoramu. Tsono Yoramu atalindira ku Ramoti Giliyadi, iye ndi Aisraele onse, chifukwa cha Hazaele mfumu ya Aramu; koma mfumu Yoramu adabwera ku Yezireele ampoletse mabala ake anamkantha Aaramu, muja adalimbana naye Hazaele mfumu ya Aramu. Nati Yehu, Ukatero mtima wanu, asapulumuke mmodzi yense kutuluka m'mudzi kukafotokozera m'Yezireele. Nayenda Yehu m'galeta, namuka ku Yezireele, popeza Yoramu anagonako; ndi Ahaziya mfumu ya Yuda anatsikira kukamuona Yoramu. Ndipo mlonda ali chilili pachilindiro m'Yezireele, naona gulu la Yehu lilinkudza, nati, Ndiona gulu. Nati Yoramu, Tenga wapakavalo, numtumize akomane nao, nanene, Mtendere kodi? Ndipo anamuka wapakavalo kukomana naye, nati, Atero mfumu, Mtendere kodi? Nati Yehu, Ngwanji mtendere, tembenukira m'mbuyo mwanga. Ndi mlonda anawafotokozera kuti, Mthenga wawafika, koma wosabwera. Pamenepo anatumiza wina wapakavalo, nawafika, nati, Atero mfumu, Mtendere kodi? Nati Yehu, Ngwanji mtendere, tembenukira m'mbuyo mwanga. Ndi mlonda anafotokozera, kuti, Wawafika, koma wosabwera; ndipo kuyendetsako kukunga kuyendetsa kwa Yehu mwana wa Nimisi, pakuti ayendetsa moyaluka. Nati Yoramu, Manga. Namanga galeta wake. Ndipo Yoramu mfumu ya Israele ndi Ahaziya mfumu ya Yuda anatuluka yense m'galeta wake, natuluka kukakomana ndi Yehu, nakomana naye pa munda wa Naboti m'Yezireele. Ndipo kunali, pamene Yoramu anaona Yehu, anati, Mtendere kodi, Yehu? Nati iye, Ngwanji mtendere pokhala chachuluka chigololo ndi nyanga zake za mai wako Yezebele? Natembenuza Yoramu manja ake, nathawa, nati kwa Ahaziya, Chiwembu, Ahaziya. Nafa nao Yehu uta wake, nalasa Yoramu pachikota, nutuluka muvi pa mtima wake, naonyezeka iye m'galeta wake. Nati Yehu kwa Bidikara kazembe wake, Mnyamule, numponye m'munda wa Naboti wa ku Yezireele; pakuti kumbukira m'mene ine ndi iwe tinali pa akavalo athu pamodzi kutsata Ahabu atate wake, Yehova anamsenzetsa katundu uyu. Ndapenyadi dzulo mwazi wa Naboti ndi mwazi wa ana ake, ati Yehova; ndipo ndikubwezera pamunda pano, ati Yehova. Mtengeni tsono, mumponye pamundapo, monga mwa mau a Yehova. Koma pochiona ichi Ahaziya mfumu ya Yuda anathawa njira ya ku Betigahani. Namtsata Yehu, nati, Mumkanthe uyonso pagaleta; namkantha pa chikweza cha Guri chili pafupi pa Ibleamu. Nathawira iye ku Megido, namwalira komweko. Ndipo anyamata ake anamnyamulira pagaleta kunka naye ku Yerusalemu, namuika ku manda ake pamodzi ndi makolo ake m'mudzi wa Davide. Ndipo pa chaka chakhumi ndi chimodzi cha Yoramu mwana wa Ahabu, Ahaziya analowa ufumu pa Yuda. Ndipo pofika Yehu ku Yezireele, Yezebele anamva, nadzikometsera m'maso, naluka tsitsi lake, nasuzumira pazenera. Ndipo polowa Yehu pachipata, mkaziyo anati, Mtendere kodi Zimiri, iwe wakupha mbuyako? Koma anakweza maso ake kuzenera, nati, Ali ndi ine ndani? Ndani? Nampenyererako adindo awiri kapena atatu. Nati iye, Mgwetsereni pansi. Namgwetsera pansi, nuwazikako mwazi wake pakhoma ndi pa akavalo, nampondereza iye pansi. Ndipo atalowa, anadya namwa, nati, Kampenyeni tsono mkazi wotembereredwa uyu, nimumuike; popeza ndiye mwana wa mfumu. Namuka iwo kuti amuike; koma sanapezeko kanthu kena koma bade, ndi mapazi, ndi zikhato za manja. Nabwerera iwo, namfotokozera. Nati iye, Ndiwo mau a Yehova ananenawo mwa mtumiki wake Eliya wa ku Tisibe, ndi kuti, Pa munda wa Yezireele agalu adzadya mnofu wa Yezebele; ndi thupi la Yezebele lidzakhala ngati ndowe pamunda m'dera la Yezireele, kuti sadzati, Ndi Yezebele uyu. Ndipo Ahabu anali nao ana amuna makumi asanu ndi awiri m'Samariya. Nalemba akalata Yehu, natumiza ku Samariya kwa akulu a Yezireele, ndiwo akuluakulu, ndi iwo adalera ana a Ahabu, ndi kuti, Tsono akakufikani inu kalata uyu, popeza muli nao ana a mbuye wanu, muli naonso magaleta ndi akavalo, ndi mudzi walinga, ndi zida, musankhe wokoma ndi woyenerayo wa ana a mbuye wanu, ndi kumuika pa mpando wachifumu wa atate wake; ndipo muiponyere nkhondo nyumba ya mbuye wanu. Koma anaopa kwambiri, nati, Taonani, mafumu awiri sanaime pamaso pake, nanga ife tidzaima bwanji? Ndipo iye wakuyang'anira nyumba, ndi iye wakuyang'anira mudzi, ndi akuluakulu, ndi iwo akulera anawo, anatumiza kwa Yehu, ndi kuti, Ife ndife akapolo anu ndi zonse mutiuza tidzachita; sitidzalonga munthu yense mfumu; chokomera pamaso panu chitani. Nawalembera kalata kachiwiri, nati, Mukakhala a ine ndi kumvera mau anga, tengani mitu ya amunawo ana a mbuye wanu, ndi kundidzera ku Yezireele mawa dzuwa lino. Koma ana a mfumu ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, anakhala ndi anthu omveka m'mudzi, amene anawalera. Ndipo kunali, powafika kalatayo, anatenga ana a mfumu, nawapha amuna makumi asanu ndi awiri, naika mitu yao m'madengu, naitumiza kwa iye ku Yezireele. Nudza mthenga, numfotokozera, kuti, Abwera nayo mitu ya ana a mfumu. Nati iye, Muiunjike miulu iwiri polowera pa chipata kufikira m'mawa. Ndipo kunali m'mawa, iye anatuluka, naima, nati kwa anthu onse, Muli olungama inu, taonani, ndinapandukira mbuye wanga ndi kumupha; koma awa onse anawakantha ndani? Dziwani tsono, kuti sikadzagwa pansi kanthu ka mau a Yehova, amene Yehova ananena za nyumba ya Ahabu; pakuti Yehova wachita chimene adanena mwa mtumiki wake Eliya. Nawakantha Yehu otsala onse a nyumba ya Ahabu m'Yezireele, ndi omveka ake onse, ndi odziwana naye, ndi ansembe ake, mpaka sanatsale wa iye ndi mmodzi yense. Pamenepo ananyamuka, nachoka, namuka ku Samariya. Ndipo pokhala kunyumba yosengera ya abusa panjira, Yehu anakomana nao abale a Ahaziya mfumu ya Yuda, nati, Ndinu ayani? Nati iwo, Ife ndife abale a Ahaziya, tilikutsika kulonjera ana a mfumu, ndi ana a nyumba yaikulu. Nati iye, Agwireni amoyo. Nawagwira amoyo, nawapha ku dzenje la nyumba yosengera, ndiwo amuna makumi anai mphambu awiri; sanasiye ndi mmodzi yense. Atachoka pamenepo, anakomana naye Yehonadabu mwana wa Rekabu wakudzamchingamira; namlonjera, nanena naye, Mtima wako ngwoongoka kodi, monga mtima wanga uvomerezana nao mtima wako? Nati Yehonadabu, Momwemo. Ukatero undipatse dzanja lako. Nampatsa dzanja lake, namkweretsa pali iye pagaleta. Nati iye, Tiye nane, ukaone changu changa cha kwa Yehova. M'mwemo anamuyendetsa m'galeta wake. Ndipo anafika ku Samariya, nakantha onse otsala a Ahabu m'Samariya, mpaka adamuononga monga mwa mau a Yehova adanenawo kwa Eliya. Ndipo Yehu anasonkhanitsa anthu onse pamodzi, nanena nao, Ahabu anatumikira Baala pang'ono, koma Yehu adzamtumikira kwambiri. Mundiitanire tsono adze kwa ine aneneri onse a Baala, ompembedza onse, ndi ansembe ake onse, asasowe mmodzi; pakuti ndili nayo nsembe yaikulu yochitira Baala; aliyense wosapenyekapo sadzakhala ndi moyo. Koma Yehu anachichita monyenga, kuti akaononge otumikira Baala. Nati Yehu, Lalikirani msonkhano wopatulika wa Baala. Naulalikira. Ndipo Yehu anatumiza kwa Aisraele onse, nadza otumikira Baala onse, wosatsala ndi mmodzi yense wosafika. Nalowa m'nyumba ya Baala; ndi nyumba ya Baala inadzala phaa. Nati kwa iye wosunga nyumba ya zovala, Tulutsira otumikira Baala onse zovala. Nawatulutsira zovala. Nalowa Yehu ndi Yehonadabu mwana wa Rekabu m'nyumba ya Baala, nati kwa otumikira Baala, Mufunefune, nimuone asakhale nanu muno otumikira Yehova, koma otumikira Baala okha. Nalowa iwo kupereka nsembe zophera ndi nsembe zopsereza. Koma Yehu adadziikira kubwalo amuna makumi asanu ndi atatu, nati, Munthu akalola wina wa anthuwa ndilikuwaika m'manja mwanu apulumuke, moyo wake kulipa moyo wake. Ndipo kunali, atatsiriza kupereka nsembe yopsereza, Yehu anati kwa otumikira ndi atsogoleri, Lowani, akantheni; asatuluke ndi mmodzi yense. Nawakantha ndi lupanga lakuthwa; ndi otumikira ndi atsogoleri anawataya kubwalo, namuka kumudzi wa nyumba ya Baala. Natulutsa zoimiritsa zija zinali m'nyumba ya Baala, nazitentha. Nagamula fano la Baala, nagamula nyumba ya Baala, naiyesa dzala mpaka lero lino. Momwemo Yehu anaononga Baala m'Israele. Koma Yehu sanazileke zoipa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene adachimwitsa nazo Israele, ndizo anaang'ombe agolide okhala m'Betele ndi m'Dani. Ndipo Yehova anati kwa Yehu, Popeza wachita bwino, pochita choongoka pamaso panga, ndi kuchitira nyumba ya Ahabu monga mwa zonse zinali m'mtima mwanga, ana ako a ku mbadwo wachinai adzakhala pa mpando wachifumu wa Israele. Koma Yehu sanasamalire kuyenda m'chilamulo cha Yehova Mulungu wa Israele ndi mtima wake wonse; sanaleke zoipa za Yerobowamu, zimene anachimwitsa nazo Israele. Masiku ao Yehova anayamba kusadza Israele; ndipo Hazaele anawakantha m'malire onse a Israele, kuyambira ku Yordani kum'mawa, dziko lonse la Giliyadi, la Agadi, ndi la Arubeni, ndi Amanase, kuyambira ku Aroere, ndiwo kumtsinje Arinoni, ndilo Giliyadi ndi Basani. Ndipo machitidwe ena a Yehu, ndi zonse anazichita, ndi mphambu yake yonse, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele? Nagona Yehu ndi makolo ake, namuika m'Samariya. Ndi Yehowahazi mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake. Ndipo masiku ake akukhala Yehu mfumu ya Israele m'Samariya ndiwo zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zitatu. Pamene Ataliya make wa Ahaziya anaona kuti mwana wake wafa, ananyamuka, naononga mbeu yonse yachifumu. Koma Yehoseba mwana wa mfumu Yoramu, mlongo wake wa Ahaziya, anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, namuba pakati pa ana a mfumu akuti aphedwe, iye ndi mlezi, nawaika m'chipinda chogonamo; nambisira Ataliya, ndipo sanaphedwe. Nakhala naye wobisika m'nyumba ya Yehova zaka zisanu ndi chimodzi; ndipo Ataliya anakhala mfumu ya dziko. Koma chaka chachisanu ndi chiwiri Yehoyada anaitanitsa atsogoleri a mazana a opha anthu, ndi a otumikira, nabwera nao kwa iye kunyumba ya Yehova, napangana nao, nawalumbiritsa m'nyumba ya Yehova, nawaonetsa mwana wa mfumu. Nawalamulira, kuti, Chochita inu ndi ichi: limodzi la magawo atatu la inu olowa pa Sabata lizilindira nyumba ya mfumu, ndi lina lizikhala ku chipata cha Suri, ndi lina ku chipata kumbuyo kwa otumikira; momwemo muzisunga nyumba, ndi kuitchinjiriza. Ndipo magawo awiri a inu, ndiwo onse otulukira pa Sabata, azilindira nyumba ya Yehova kuzinga mfumu. Ndipo muzizinga mfumu, yense zida zake m'manja mwake, ndi iye wakulowa poima inupo aphedwe; ndipo muzikhala inu ndi mfumu potuluka ndi polowa iye. Ndipo atsogoleri a mazana anachita monga mwa zonse anawalamulira Yehoyada wansembe, natenga yense anthu ake olowera pa Sabata, ndi otulukira pa Sabata, nafika kwa Yehoyada wansembeyo. Ndipo wansembeyo anapereka kwa atsogoleri a mazana mikondo ndi zikopa, zinali za mfumu Davide, zosungika m'nyumba ya Yehova. Ndipo otumikira anakhala chilili yense ndi zida zake m'manja mwake, kuyambira mbali ya kulamanja kufikira mbali ya kulamanzere ya nyumbayo, ku guwa la nsembe, ndi kunyumba, kuzinga mfumu. Atatero, anatulutsa mwana wa mfumu, namuika korona, nampatsa buku la umboni, namlonga ufumu, namdzoza, naomba m'manja, nati, Mfumu ikhale ndi moyo. Pamene Ataliya anamva phokoso la otumikira ndi anthu, anadza kwa anthu m'nyumba ya Yehova; napenya, ndipo taonani, mfumu ili chilili pachiundo, monga ankachita, ndi atsogoleri ndi amalipenga pali mfumu; nakondwerera anthu onse a m'dziko, naomba malipenga. Pamenepo Ataliya anang'amba zovala zake, nafuula Chiwembu, Chiwembu. Koma Yehoyada wansembe analamulira atsogoleri a mazana oyang'anira khamu, nanena nao, Mumtulutse mkaziyo pabwalo pakati pa mipambo; womtsata iye mumuphe ndi lupanga; pakuti wansembe adati, Asaphedwe m'nyumba ya Yehova. Ndipo anamgwira, napita naye njira yolowera akavalo kunyumba ya mfumu, namupha pomwepo. Ndipo Yehoyada anachita chipangano pakati pa Yehova ndi mfumu ndi anthu, akhale anthu a Yehova; pakati pa mfumunso ndi anthu. Namuka anthu onse a m'dzikomo kunyumba ya Baala, naigumula; maguwa ake a nsembe ndi mafano ake anawaswaiswa, napha Matani wansembe wa Baala ku maguwa a nsembe. Ndipo wansembeyo anaika oyang'anira nyumba ya Yehova. Napita nao atsogoleri a mazana, ndi opha anthu, ndi otumikira, ndi anthu onse a m'dziko; ndipo iwo anatsika nayo mfumu kunyumba ya Yehova, nadzera njira ya chipata cha otumikira, kunka kunyumba ya mfumu. Nakhala iye pa chimpando cha mafumu. Nakondwerera anthu onse a m'dziko, ndi m'mudzi munali phee; ndipo adapha Ataliya ndi lupanga kunyumba ya mfumu. Yowasi anali wa zaka zisanu ndi ziwiri polowa iye ufumu. Chaka chachisanu ndi chiwiri cha Yehu, Yowasi analowa ufumu wake; nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi anai; ndi dzina la mai wake ndiye Zibiya wa ku Beereseba. Ndipo Yowasi anachita zoongoka pamaso pa Yehova masiku ake onse, m'mene anamlangizira wansembe Yehoyada. Koma misanje sanaichotse; anthu anapherabe nsembe, nafukiza kumisanje. Ndipo Yowasi anati kwa ansembe, Landirani ndalama zonse za zinthu zopatulika azibwera nazo kunyumba ya Yehova, ndizo ndalama za otha msinkhu, ndalama za munthu aliyense monga adamuyesa, ndi ndalama zimene yense azikumbuka m'mtima mwake kuti abwere nazo kunyumba ya Yehova. Ansembe azilandire yense kwa iye amene adziwana naye, akonze nazo mogamuka nyumba, paliponse akapeza pogamuka. Koma kunali, chaka cha makumi awiri mphambu zitatu cha mfumu Yowasi, ansembe sanathe kukonza mogamuka nyumba. Pamenepo mfumu Yowasi anaitana Yehoyada wansembe, ndi ansembe ena, nanena nao, Mulekeranji kukonza mogamuka nyumba? Tsono musalandiranso ndalama kwa anzanu odziwana nao, kuziperekera mogamuka nyumba. Navomera ansembe kusalandiranso ndalama za anthu, kapena kukonza mogamuka nyumba. Ndipo Yehoyada wansembe anatenga bokosi, naboola chiboo pa chivundikiro chake, naliika pafupi pa guwa la nsembe, ku dzanja lamanja polowera nyumba ya Yehova; ndipo ansembe akusunga pakhomo anaikamo ndalama zonse anabwera nazo anthu kunyumba ya Yehova. Ndipo pakuona kuti ndalama zidachuluka m'bokosimo, anakwerako mlembi wa mfumu, ndi mkulu wa ansembe, nazimanga m'matumba, naziyesa ndalama zopereka m'nyumba ya Yehova. Napereka ndalama zoyesedwa m'manja mwa iwo akuchita ntchitoyi, akuyang'anira nyumba ya Yehova; ndipo iwo analipira nazo amisiri a mitengo ndi omanga, akugwira ntchito ya pa nyumba ya Yehova, ndi omanga miyala ndi osema miyala, ndi kugula mitengo ndi miyala yosema kukakonza mogamuka nyumba ya Yehova, ndi zonse zoigulira nyumba zoikonzera. Koma sanapangire nyumba ya Yehova mbale zasiliva, mbano, mbale zowazira, malipenga, zotengera zilizonse zagolide, kapena zotengera zilizonse zasiliva, kuzipanga ndi ndalama adabwera nazo kunyumba ya Yehova; pakuti anazipereka kwa iwo akugwira ntchitoyi, nakonza nazo nyumba ya Yehova. Ndipo sanawerengere anthu, amene anapereka ndalamazi m'manja mwao kuti apatse ogwira ntchito; popeza anachita mokhulupirika. Ndalama za nsembe zopalamula ndi ndalama za nsembe yauchimo sanabwere nazo kunyumba ya Yehova; nza ansembe izi. Pamenepo Hazaele mfumu ya Aramu anakwera, nathira nkhondo pa Gati, naulanda, nalunjikitsa nkhope yake kukwera ku Yerusalemu. Koma Yowasi mfumu ya Yuda anatenga zopatulika zonse adazipatula Yehosafati, ndi Yehoramu, ndi Ahaziya, makolo ake, mafumu a Yuda, ndi zopatulika zakezake, ndi golide yense anampeza pa chuma cha nyumba ya Yehova, ndi cha nyumba ya mfumu, nazitumiza kwa Hazaele mfumu ya Aramu; motero anabwerera kuchoka ku Yerusalemu. Machitidwe ena tsono a Yowasi ndi zonse adazichita sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda? Ndipo anyamata ake ananyamuka, napangana, nakantha Yowasi kunyumba ya Milo potsikira ku Sila. Pakuti Yozakara mwana wa Simeati, ndi Yehozabadi mwana wa Somere, anyamata ake, anamkantha, nafa iye; ndipo anamuika kwa makolo ake m'mudzi wa Davide; ndi Amaziya mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake. Chaka cha makumi awiri ndi zitatu cha Yowasi mwana wa Ahaziya mfumu ya Yuda, Yehowahazi mwana wa Yehu analowa ufumu wake wa Israele ku Samariya, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri. Nachita choipa pamaso pa Yehova, natsata zolakwa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele; sanazileke. Ndipo mkwiyo wa Yehova unayaka pa Israele, nawapereka m'dzanja la Hazaele mfumu ya Aramu, ndi m'dzanja la Benihadadi mwana wa Hazaele, masiku onsewo. Koma Yehowahazi anapembedza Yehova, Yehova namvera; pakuti anapenya kupsinjika kwake kwa Israele m'mene mfumu ya Aramu inawapsinja. Ndipo Yehova anapatsa Israele mpulumutsi, natuluka iwo pansi pa dzanja la Aaramu; nakhala ana a Israele m'mahema mwao monga kale. Komatu sanalekane nazo zolakwa za nyumba ya Yerobowamu, zimene analakwitsa nazo Israele, nayenda m'mwemo; nichitsalanso chifanizo m'Samariya. Koma mfumu ya Aramu sanasiyire Yehowahazi anthu, koma apakavalo makumi asanu, ndi magaleta khumi, ndi oyenda pansi zikwi khumi; popeza mfumu ya Aramu anawaononga, nawayesa ngati fumbi lopondapo. Machitidwe ena tsono a Yehowahazi, ndi zonse anazichita, ndi mphamvu yake, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele? Ndipo Yehowahazi anagona ndi makolo ake, namuika m'Samariya; nakhala mfumu m'malo mwake Yowasi mwana wake. Chaka cha makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri cha Yowasi mfumu ya Yuda, Yehowasi mwana wa Yehowahazi analowa ufumu wake wa Israele m'Samariya, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi. Nachita choipa pamaso pa Yehova, osazileka zolakwa zonse za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele, koma anayendamo. Machitidwe ena tsono a Yowasi, ndi zonse anazichita, ndi mphamvu yake yochita nkhondo nayo pa Amaziya mfumu ya Yuda, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele? Ndipo Yowasi anagona ndi makolo ake, ndi Yerobowamu anakhala pa mpando wachifumu wake; namuika Yowasi m'Samariya pamodzi ndi mafumu a Israele. Ndipo Elisa anadwala nthenda ija adafa nayo, namtsikira Yowasi mfumu ya Israele, namlirira, nati, Atate wanga, atate wanga, galeta wa Israele ndi apakavalo ake! Nanena naye Elisa, Tenga uta ndi mivi; nadzitengera uta ndi mivi. Nati kwa mfumu ya Israele, Pingiridzani. Napingiridza. Ndipo Elisa anasanjika manja ake pa manja a mfumu. Nati, Tsegulani zenera la kum'mawa. Nalitsegula. Nati Elisa, Ponyani. Naponya. Nati iye, Muvi wa chipulumutso wa Yehova ndiwo muvi wa kukupulumutsani kwa Aaramu; popeza mudzakantha Aaramu m'Afeki mpaka mudzawatha. Nati iye, Tengani mivi; naitenga. Nati kwa mfumu ya Israele, Kwapula pansi; nakwapula katatu, naleka. Nakwiya naye munthu wa Mulungu, nati, Mukadakwapula kasanu, kapena kasanu ndi kamodzi; mukadatero, mukadadzakantha Aaramu mpaka kuwatha; koma tsopano mudzawakantha Aaramu katatu kokha. Pamenepo Elisa anamwalira, ndipo anamuika. Ndipo magulu a Amowabu analowa m'dziko poyambira chaka. Ndipo anthu, pakuika maliro a munthu wina, anaona gulu la nkhondo, naponya mtembo m'manda mwa Elisa; koma pamene mtembowo unakhudza mafupa a Elisa, wakufayo anauka, naima chilili. Ndipo Hazaele mfumu ya Aramu anapsinja Israele masiku onse a Yehowahazi. Koma Yehova analeza nao mtima, nawachitira chifundo, nawatembenukira; chifukwa cha chipangano chake ndi Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, wosafuna kuwaononga, kapena kuwatayiratu pankhope pake. Nafa Hazaele mfumu ya Aramu, nakhala mfumu m'malo mwake Benihadadi mwana wake. Ndi Yehowasi mwana wa Yehowahazi analandanso m'dzanja la Benihadadi mwana wa Hazaele midzi ija adailanda m'dzanja la Yoahazi atate wake ndi nkhondo. Yowasi anamkantha katatu, naibweza midzi ya Israele. Chaka chachiwiri cha Yehowasi mwana wa Yehowahazi mfumu ya Israele, Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda analowa ufumu wake. Ndiye wa zaka makumi awiri ndi zisanu polowa ufumu; nakhala mfumu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai m'Yerusalemu; dzina la make ndiye Yehowadani wa ku Yerusalemu. Ndipo anachita zoongoka pamaso pa Yehova, koma wosanga Davide kholo lake; nachita monga mwa zonse anazichita Yowasi atate wake. Koma misanje sanaichotse; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje. Ndipo kunali, utakhazikika ufumu m'dzanja lake, anakantha anyamata ake amene adakantha mfumu atate wake; koma ana a ambandawo sanawaphe, monga mwalembedwa m'buku la chilamulo cha Mose, m'mene adalamulira Yehova, ndi kuti, Atate asaphedwere ana, kapena ana kuphedwera atate; koma yense afere kulakwa kwa iye yekha. Anapha Aedomu m'Chigwa cha Mchere zikwi khumi, nalanda Sela ndi nkhondo, nautcha dzina lake Yokotele mpaka lero lino. Pamenepo Amaziya anatuma mithenga kwa Yehowasi mwana wa Yehowahazi mwana wa Yehu mfumu ya Israele, ndi kuti, Idzani tionane maso. Natumiza Yehowasi mfumu ya Israele kwa Amaziya mfumu ya Yuda, ndi kuti, Mtungwi wa ku Lebanoni unatumiza mau kwa mkungudza wa ku Lebanoni, ndi kuti, Mpatse mwana wanga wamwamuna mwana wako wamkazi akhale mkazi wake; ndipo inapitapo nyama ya kuthengo ya ku Lebanoni, nipondereza mtungwiwo. Wakanthadi Aedomu, koma mtima wako wakukweza; ulemekezeke, nukhale kwanu; udziutsiranji tsoka, ungagwe iwe ndi Yuda pamodzi nawe; Koma Amaziya sanamvere. Motero anakwera Yehowasi mfumu ya Israele, ndipo iye ndi Amaziya mfumu ya Yuda anapenyana maso ku Betesemesi, ndiwo wa Yuda. Nakanthidwa Yuda pamaso pa Israele, nathawira yense kuhema kwake. Ndipo Yehowasi mfumu ya Israele anagwira Amaziya mfumu ya Yuda, mwana wa Yowasi mwana wa Ahaziya, ku Betesemesi, nadza ku Yerusalemu, nagamula linga la Yerusalemu kuyambira chipata cha Efuremu kufikira chipata cha kungodya, mikono mazana anai. Natenga golide ndi siliva yense, ndi zotengera zonse anazipeza m'nyumba ya Yehova, ndi ku chuma cha m'nyumba ya mfumu, achikole omwe; nabwera kunka ku Samariya. Machitidwe ena tsono a Yehowasi adazichita, ndi mphamvu yake, ndi umo analimbana naye Amaziya mfumu ya Yuda, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele? Nagona Yehowasi ndi makolo ake, namuika m'Samariya pamodzi ndi mafumu a Israele; nakhala mfumu m'malo mwake Yerobowamu mwana wake. Ndipo Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda anakhala ndi moyo, atamwalira Yehowasi mwana wa Yehowahazi mfumu ya Israele, zaka khumi ndi zisanu. Machitidwe ena tsono a Amaziya, sanalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda? Ndipo anamchitira chiwembu m'Yerusalemu, nathawira iye ku Lakisi; koma anatumiza akumtsata ku Lakisi, namupha komweko. Nabwera naye pa akavalo, namuika ku Yerusalemu pamodzi ndi makolo ake m'mudzi wa Davide. Ndipo anthu onse a Yuda anatenga Azariya, (ndiye Uziya), ndiye wa zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi, namlonga ufumu m'malo mwa atate wake Amaziya. Anamanga Elati, naubweza kwa Yuda, mfumuyo itagona ndi makolo ake. Chaka chakhumi ndi zisanu cha Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda, Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele analowa ufumu wake m'Samariya, nakhala mfumu zaka makumi anai mphambu chimodzi. Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, sanaleke zolakwa zonse za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele. Anabweza malire a Israele kuyambira polowera ku Hamati mpaka ku Nyanja ya Araba, monga mwa mau a Yehova Mulungu wa Israele, amene ananena ndi dzanja la mtumiki wake Yona mwana wa Amitai mneneriyo, ndiye wa Gatihefere. Pakuti Yehova anapenya kuti kuzunzika kwao kwa Israele nkowawa ndithu; popeza panalibe womangika kapena womasuka, ndipo panalibe womthandiza Israele. Ndipo Yehova sadanena kuti adzafafaniza dzina la Israele pansi pa thambo; koma anawapulumutsa ndi dzanja la Yerobowamu mwana wa Yowasi. Machitidwe ena tsono a Yerobowamu, ndi zonse anazichita, ndi mphamvu yake, umo anachita nkhondo, nabweza kwa Israele Damasiko ndi Hamati amene anali a Yuda, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele? Ndipo Yerobowamu anagona ndi makolo ake, ndiwo mafumu a Israele; nakhala mfumu m'malo mwake Zekariya mwana wake. Chaka cha makumi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri cha Yerobowamu mfumu ya Israele, Azariya mwana wa Amaziya mfumu ya Yuda analowa ufumu wake. Anali wa zaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka makumi asanu mphambu ziwiri m'Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Yekoliya wa ku Yerusalemu. Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazichita atate wake Amaziya. Komatu sanaichotse misanje; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje. Ndipo Yehova anadwaza mfumu, nakhala iye wakhate mpaka tsiku la imfa yake, nakhala m'nyumba ya padera. Ndipo Yotamu mwana wa mfumu anayang'anira banja la mfumu, naweruza anthu a m'dziko. Machitidwe ena tsono a Azariya, ndi zonse anazichita, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda? Nagona Azariya ndi makolo ake, namuika ndi makolo ake m'mudzi wa Davide; nakhala mfumu m'malo mwake Yotamu mwana wake. Chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu cha Azariya mfumu ya Yuda, Zekariya mwana wa Yerobowamu anakhala mfumu ya Israele m'Samariya miyezi isanu ndi umodzi. Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga adachita makolo ake; sanaleke zolakwa zake za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele. Ndipo Salumu mwana wa Yabesi anamchitira chiwembu, namkantha pamaso pa anthu, namupha; nakhala mfumu m'malo mwake. Machitidwe ena tsono a Zekariya, taonani, zalembedwa m'buku la machitidwe a mafumu a Israele. Awa ndi mau a Yehova anawanena ndi Yehu, ndi kuti, Ana ako kufikira mbadwo wachinai adzakhala pa mpando wachifumu wa Israele. Ndipo kunatero momwemo. Salumu mwana wa Yabesi analowa ufumu wake chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zinai cha Uziya mfumu ya Yuda, nakhala mfumu mwezi umodzi m'Samariya. Koma anakwera Menahemu mwana wa Gadi kuchokera ku Tiriza, nafika ku Samariya, nakantha Salumu mwana wa Yabesi m'Samariya, namupha; nakhala mfumu m'malo mwake. Machitidwe ena tsono a Salumu ndi chiwembu chake anachichita, taonani, zalembedwa m'buku la machitidwe a mafumu a Israele. Pamenepo Menahemu anakantha Tapuwa, ndi onse anali m'mwemo, ndi malire ake kuyambira ku Tiriza; popeza sanamtsegulire pachipata; anaukantha, natumbula akazi onse a pakati okhala m'mwemo. Chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zinai cha Azariya mfumu ya Yuda, Menahemu mwana wa Gadi analowa ufumu wake wa Israele, nakhala mfumu zaka khumi m'Samariya. Nachita choipa pamaso pa Yehova masiku ake onse, osaleka zolakwa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele. Pamenepo Pulo mfumu ya Asiriya anadza kudzamenyana ndi dziko, koma Menahemu anampatsa Pulo matalente a siliva chikwi chimodzi; kuti dzanja lake likhale naye kukhazikitsa ufumu m'dzanja lake. Ndipo Menahemu anasonkhetsa Israele ndalamazi, nasonkhetsa achuma, yense masekeli makumi asanu a siliva, kuti azipereke kwa mfumu ya Asiriya. Nabwerera mfumu ya Asiriya osakhala m'dzikomo. Machitidwe ena tsono a Menahemu, ndi zonse anazichita, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele? Nagona Menahemu ndi makolo ake; nakhala mfumu m'malo mwake Pekahiya mwana wake. Chaka cha makumi asanu a Azariya mfumu ya Yuda, Pekahiya mwana wa Menahemu analowa ufumu wake wa Israele m'Samariya, nakhala mfumu zaka ziwiri. Nachita choipa pamaso pa Yehova, sanaleke zolakwa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele. Ndipo Peka mwana wa Remaliya, kazembe wake, anamchitira chiwembu, nawakantha limodzi mfumu ndi Arigobu ndi Ariye m'Samariya, m'nsanja ya kunyumba ya mfumu; pamodzi ndi iye panali amuna makumi asanu a Giliyadi; ndipo anamupha, nakhala mfumu m'malo mwake. Machitidwe ena tsono a Pekahiya ndi zonse anazichita, taonani zalembedwa m'buku la machitidwe a mafumu a Israele. Chaka cha makumi asanu mphambu ziwiri cha Azariya mfumu ya Yuda, Peka mwana wa Remaliya analowa ufumu wake wa Israele m'Samariya, nakhala mfumu zaka makumi awiri. Nachita choipa pamaso pa Yehova, osaleka zolakwa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele. Masiku a Peka mfumu ya Israele anadza Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, nalanda Iyoni, ndi Abele-Beti-Maaka, ndi Yanowa, ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Giliyadi, ndi Galileya, dziko lonse la Nafutali; nawatenga andende kunka nao ku Asiriya. Ndipo Hoseya mwana wa Ela anamchitira chiwembu Peka mwana wa Remaliya, namkantha, namupha, nakhala mfumu m'malo mwake chaka cha makumi awiri cha Yotamu mwana wa Uziya. Machitidwe ena tsono a Peka, ndi zonse anazichita, taonani, zalembedwa m'buku la machitidwe a mafumu a Israele. Chaka chachiwiri cha Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Israele, Yotamu mwana wa Uziya mfumu ya Yuda analowa ufumu wake. Ndiye wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi m'Yerusalemu; ndipo dzina la make ndiye Yerusa mwana wa Zadoki. Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova; anachita monga mwa zonse anazichita atate wake Uziya. Komatu sanaichotse misanje; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje. Iye anamanga chipata cha kumtunda cha nyumba ya Yehova. Machitidwe ena tsono a Yotamu, ndi zonse anazichita, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda? Masiku awa Yehova anayamba kutumizira Yuda Rezini mfumu ya Aramu, ndi Peka mwana wa Remaliya, amenyane naye. Ndipo anagona Yotamu ndi makolo ake, namuika pamodzi ndi makolo ake m'mudzi wa Davide kholo lake; nakhala mfumu m'malo mwake Ahazi mwana wake. Chaka chakhumi mphambu zisanu ndi ziwiri cha Peka mwana wa Remaliya Ahazi mwana wa Yotamu mfumu ya Yuda analowa ufumu wake. Ahazi anali wa zaka makumi awiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi m'Yerusalemu; koma sanachite zoongoka pamaso pa Yehova Mulungu wake, ngati Davide kholo lake; popeza anayenda m'njira ya mafumu a Israele, napititsanso mwana wake pamoto, monga mwa zonyansa za amitundu amene Yehova anawaingitsa pamaso pa ana a Israele. Ndipo anaphera nsembe, nafukiza zonunkhira kumisanje, ndi kuzitunda, ndi patsinde pa mtengo uliwonse wogudira. Pamenepo Rezini mfumu ya Aramu, ndi Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Israele, anakwera kunka ku Yerusalemu kukachita nkhondo, nammangira Ahazi misasa; koma sanakhoze kumgonjetsa. Nthawi yomweyo Rezini mfumu ya Aramu anabwezera Elati kwa Aramu, napirikitsa Ayuda ku Elati; nadza Aaramu ku Elati, nakhala komwemo kufikira lero lino. Ndipo Ahazi anatuma mithenga kwa Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, ndi kuti, Ine ndine kapolo wanu ndi mwana wanu; kwerani, mudzandipulumutse m'dzanja la mfumu ya Aramu, ndi m'dzanja la mfumu ya Israele anandiukirawo. Natenga Ahazi siliva ndi golide wopezeka m'nyumba ya Yehova, ndi ku chuma cha nyumba ya mfumu, nazitumiza mtulo kwa mfumu ya Asiriya. Nimmvera mfumu ya Asiriya, nikwera kunka ku Damasiko mfumu ya Asiriya, niulanda, nipita nao anthu ake andende ku Kiri, nimupha Rezini. Ndipo mfumu Ahazi anamuka ku Damasiko kukakomana ndi Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, naona guwa la nsembe linali ku Damasiko; natumiza mfumu Ahazi kwa Uriya wansembe chithunzithunzi chake, ndi chifanizo chake, monga mwa mamangidwe ake onse. Ndipo Uriya wansembe anamanga guwa la nsembelo, monga mwa zonse anazitumiza mfumu Ahazi zochokera ku Damasiko; momwemo Uriya wansembe analimanga asanabwere mfumu ku Damasiko. Atafika mfumu kuchokera ku Damasiko, anapenya mfumu guwa la nsembelo, nayandikiza mfumu ku guwa la nsembelo, napereka nsembe pomwepo. Nafukiza nsembe yake yopsereza ndi nsembe yake yaufa, natsanulira nsembe yake yothira, nawaza mwazi wa nsembe zake zamtendere pa guwa la nsembelo. Nalichotsa guwa la nsembe lamkuwa linali pamaso pa Yehova, nalichotsa ku khomo la nyumba pakati pa guwa la nsembe lake ndi nyumba ya Yehova, naliika kumpoto kwa guwa la nsembe lake. Ndipo mfumu Ahazi analamulira Uriya wansembe, kuti, Pa guwa la nsembe lalikulu uzifukiza nsembe yopsereza yam'mawa, ndi nsembe yaufa yamadzulo, ndi nsembe yopsereza ya mfumu, ndi nsembe yake yaufa, pamodzi ndi nsembe yopsereza ya anthu onse a m'dziko, ndi nsembe yao yaufa, ndi nsembe zao zothira; uziwaza pa ilo mwazi wonse wa nsembe yopsereza, ndi mwazi wonse wa nsembe yophera; koma guwa la nsembe lamkuwa ndi langa, lofunsira nalo. Nachita Uriya wansembe monga mwa zonse adalamulira mfumu Ahazi. Ndipo mfumu Ahazi anadula matsekerezo a maphaka, nachotsa mbiya pamwamba pao, natsitsa thawale pamwamba pa ng'ombe zamkuwa zili pansi pake, naziika pa chiunda chamiyala. Nachotsa kunyumba ya Yehova malo ophimbika a pa Sabata adawamanga kunyumba, ndi polowera mfumu pofuma kunja, chifukwa cha mfumu ya Asiriya. Machitidwe ena tsono adawachita Ahazi, sanalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda? Nagona Ahazi ndi makolo ake, namuika ndi makolo ake m'mudzi wa Davide; nakhala mfumu m'malo mwake Hezekiya mwana wake. Chaka chakhumi ndi ziwiri cha Ahazi mfumu ya Yuda Hoseya mwana wa Ela analowa ufumu wake wa Israele m'Samariya, nakhala mfumu zaka zisanu ndi zinai. Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, koma osati monga mafumu a Israele asanakhale iye. Anamkwerera Salimanezere mfumu ya Asiriya kumthira nkhondo; ndipo Hoseya anamgonjera, namsonkhera mitulo. Koma mfumu ya Asiriya anampeza Hoseya alikuchita chiwembu; popeza anatuma mithenga kwa So mfumu ya ku Ejipito, osaperekanso mtulo kwa mfumu ya Asiriya, monga akachita chaka ndi chaka; chifukwa chake mfumu ya Asiriya anamtsekera, nammanga m'kaidi. Pamenepo mfumu ya Asiriya anakwera m'dziko monse, nakwera ku Samariya, naumangira misasa zaka zitatu. Chaka chachisanu ndi chinai cha Hoseya mfumu ya Asiriya analanda Samariya, natenga Aisraele andende, kunka nao ku Asiriya; nawakhalitsa m'Hala, ndi m'Habori, ku mtsinje wa Gozani, ndi m'midzi ya Amedi. Kudatero, popeza ana a Israele adachimwira Yehova Mulungu wao, amene anawakweza kuwatulutsa m'dziko la Ejipito pansi pa dzanja la Farao mfumu ya Aejipito, ndipo anaopa milungu ina, nayenda m'miyambo ya amitundu amene Yehova adawaingitsa pamaso pa ana a Israele, ndi m'miyambo ya mafumu a Israele imene iwo anawalangiza. Ndipo ana a Israele anachita m'tseri zinthu zosayenera pa Yehova Mulungu wao, nadzimangira misanje m'midzi mwao monse kunsanja ya olonda ndi kumudzi walinga komwe. Nadziimikira zoimiritsa ndi zifanizo pa chitunda chilichonse chachitali, ndi patsinde pa mtengo uliwonse wogudira; nafukizapo zonunkhira pa misanje yonse, monga umo amachitira amitundu amene Yehova adawachotsa pamaso pao, nachita zoipa kuutsa mkwiyo wa Yehova; natumikira mafano amene Yehova anawanena nao, Musachita ichi. Ndipo Yehova anachitira umboni Israele ndi Yuda mwa dzanja la mneneri aliyense, ndi mlauli aliyense, ndi kuti, Bwererani kuleka ntchito zanu zoipa, nimusunge malamulo anga ndi malemba anga, monga mwa chilamulo chonse ndinachilamulira makolo anu, ndi kuchitumizira inu mwa dzanja la atumiki anga aneneri. Koma sanamvere, naumitsa khosi lao, monga khosi la makolo ao amene sanakhulupirire Yehova Mulungu wao. Ndipo anakaniza malemba ake, ndi chipangano anachichita ndi makolo ao, ndi mboni zake anawachitira umboni nazo, natsata zopanda pake, nasanduka opanda pake, natsata amitundu owazinga, amene Yehova adawalamulira nao, kuti asachite monga iwowa. Ndipo anasiya malamulo onse a Yehova Mulungu wao, nadzipangira mafano oyenga, anaang'ombe awiri, napanga chifanizo, nagwadira khamu lonse la kuthambo, natumikira Baala. Napititsa ana ao aamuna ndi aakazi kumoto, naombeza ula, nachita zanyanga, nadzigulitsa kuchita choipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wake. Chifukwa chake Yehova anakwiya naye Israele kwakukulu, nawachotsa pamaso pake osatsala mmodzi, koma fuko la Yuda lokha. Yudanso sanasunge malamulo a Yehova Mulungu wao, koma anayenda m'malemba a Israele amene adawaika. Ndipo Yehova anakaniza mbumba yonse ya Israele, nawazunza, nawapereka m'dzanja la ofunkha, mpaka anawataya pamaso pake. Pakuti anang'amba Israele, kumchotsa kunyumba ya Davide; ndipo anamlonga mfumu Yerobowamu mwana wa Nebati; Yerobowamu naingitsa Israele asatsate Yehova, nawalakwitsa kulakwa kwakukulu. Nayenda ana a Israele m'zolakwa zonse za Yerobowamu, zimene anazichita osazileka; mpaka Yehova adachotsa Israele pamaso pake, monga adanena mwa dzanja la atumiki ake onse aneneriwo. Momwemo Israele anachotsedwa m'dziko lao kunka nao ku Asiriya mpaka lero lino. Ndipo mfumu ya Asiriya anabwera nao anthu ochokera ku Babiloni, ndi ku Kuta, ndi ku Ava, ndi ku Hamati, ndi ku Sefaravaimu, nawakhalitsa m'midzi ya Samariya, m'malo mwa ana a Israele; nakhala iwo eni ake a Samariya, nakhala m'midzi mwake. Ndipo kunali, poyamba iwo kukhala komweko, sanaope Yehova; ndipo Yehova anawatumizira mikango, niwapha ena a iwowa. Motero ananena ndi mfumu ya Asiriya, kuti, Amitundu aja mudawachotsa kwao, ndi kuwakhalitsa m'midzi ya Samariya, sadziwa makhalidwe a Mulungu wa dzikoli; chifukwa chake anawatumizira mikango pakati pao, ndipo taonani, ilikuwapha; popeza sadziwa makhalidwe a Mulungu wa dzikoli. Pamenepo mfumu ya Asiriya analamulira, kuti, Mukani naye komweko wina wa ansembe munawachotsako, nakakhale komweko, akawalangize makhalidwe a Mulungu wa dzikoli. Nadza wina wa ansembewo adawachotsa ku Samariya, nakhala ku Betele, nawalangiza m'mene azimuopera Yehova. Koma a mtundu uliwonse anapanga milungu yaoyao, naiika m'nyumba za misanje adazimanga Asamariya, a mtundu uliwonse m'midzi mwao mokhala iwo. Ndipo anthu a Babiloni anapanga Sukoti-Benoti, ndi anthu a Kuta anapanga Neregali, ndi anthu a Hamati anapanga Ashima, ndi Aavi anapanga Nibihazi ndi Taritaki; ndi a Sefaravaimu anawatentha ana ao m'moto kwa Adrameleki, ndi Anameleki, milungu ya Asefaravaimu. Popeza anaopanso Yehova, anadziikira mwa iwo okha ansembe a misanje, ndiwo anaperekera nsembe m'nyumba za misanje. Amaopa Yehova, namatumikiranso milungu yao, monga mwa miyambo ya amitundu anawachotsako. Mpaka lero lino achita monga mwa miyambo yoyambayi; saopa Yehova, sachita monga mwa malemba ao, kapena maweruzo ao, kapena chilamulo, kapena choikika adachilamulira Yehova ana a Yakobo, amene anamutcha Israele, ndiwo amene Yehova adapangana nao, nawalamulira, ndi kuti, Musamaopa milungu ina, kapena kuigwadira, kapena kuitumikira, kapena kuiphera nsembe; koma Yehova amene anakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito ndi mphamvu yaikulu, ndi dzanja lotambasuka, Iyeyu muzimuopa, ndi Iyeyu muzimgwadira, ndi Iyeyu muzimphera nsembe; ndi malemba, ndi maweruzo, ndi chilamulo, ndi choikika anakulemberani muzisamalira kuzichita masiku onse, nimusamaopa milungu ina; ndi chipangano ndinachichita nanu musamachiiwala, kapena kuopa milungu ina iai; koma Yehova Mulungu wanu muzimuopa, nadzakulanditsani Iyeyu m'dzanja la adani anu onse. Koma sanamvere, nachita monga mwa mwambo wao woyamba. Ndipo amitundu awa anaopa Yehova, natumikira mafano ao osema; ana ao omwe, ndi zidzukulu zao zomwe, monga anachita makolo ao, momwemo iwo omwe mpaka lero lino. Ndipo kunali chaka chachitatu cha Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israele, Hezekiya mwana wa Ahazi mfumu ya Yuda analowa ufumu wake. Ndiye wa zaka makumi awiri ndi zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai m'Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Abi mwana wa Zekariya. Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazichita Davide kholo lake. Anachotsa misanje, naphwanya zoimiritsa, nalikha chifanizo, naphwanya njoka ija yamkuwa adaipanga Mose; pakuti kufikira masiku awa ana a Israele anaifukizira zonunkhira, naitcha Chimkuwa. Anakhulupirira Yehova Mulungu wa Israele; atafa iye panalibe wakunga iye mwa mafumu onse a Yuda, ngakhale mwa iwo okhalapo asanabadwe iye. Pakuti anaumirira Yehova osapatuka pambuyo pake, koma anasunga malamulo amene Yehova adawalamulira Mose. Ndipo Yehova anali naye, nachita iye mwanzeru kulikonse anamukako, napandukira mfumu ya Asiriya osamtumikira. Anakantha Afilisti mpaka Gaza ndi malire ake, kuyambira nsanja ya olonda mpaka mudzi walinga. Ndipo kunali chaka chachinai cha mfumu Hezekiya, ndicho chaka chachisanu ndi chiwiri cha Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israele Salimanezere mfumu ya Asiriya anakwerera Samariya, naumangira misasa. Pakutha pake pa zaka zitatu anaulanda, ndicho chaka chachisanu ndi chimodzi cha Hezekiya, ndicho chaka chachisanu ndi chinai cha Hoseya mfumu ya Israele analanda Samariya. Ndipo mfumu ya Asiriya anachotsa Aisraele kunka nao ku Asiriya, nawakhalitsa m'Hala, ndi m'Habori, ku mtsinje wa Gozani, ndi m'midzi ya Amedi; chifukwa sanamvere mau a Yehova Mulungu wao, koma analakwira chipangano chake, ndicho zonse anazilamulira Mose mtumiki wa Yehova; sanazimvere kapena kuzichita. Chaka chakhumi ndi zinai cha Hezekiya Senakeribu mfumu ya Asiriya anakwerera midzi yonse ya malinga ya Yuda, nailanda. Natumiza Hezekiya mfumu ya Yuda kwa mfumu ya Asiriya ku Lakisi, ndi kuti, Ndalakwa; mundichokere; chimene mundisenzetse ndisenza. Pamenepo mfumu ya Asiriya anaikira Hezekiya mfumu ya Yuda matalente mazana atatu a siliva ndi matalente makumi atatu a golide. Napereka Hezekiya siliva yense wopezeka m'nyumba ya Yehova, ndi ku chuma cha nyumba ya mfumu. Nthawi yomweyi Hezekiya anakanganula golide wa pa zitseko za Kachisi wa Yehova, ndi pa zimphuthu adazikuta Hezekiya mfumu ya Yuda, nampereka kwa mfumu ya Asiriya. Ndipo mfumu ya Asiriya anatuma nduna ndi mkulu wa adindo ndi kazembe ochokera ku Lakisi ndi khamu lalikulu la nkhondo kwa mfumu Hezekiya ku Yerusalemu. Nakwera iwo, nafika ku Yerusalemu. Ndipo atakwera, anafika, naima kumcherenje wa thamanda la kumtunda, ndilo la ku mseu wa ku mwaniko wa otsuka nsalu. Ndipo m'mene adaitana mfumu, anawatulukira Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyang'anira nyumba ya mfumu, ndi Sebina mlembi, ndi Yowa mwana wa Asafu wolemba mbiri. Nanena nao kazembeyo, Muuzetu Hezekiya, Itero mfumu yaikulu, mfumu ya Asiriya, Chikhulupiriro ichi nchotani uchikhulupirira? Ukuti koma ndiwo mau a pakamwa pokha, Pali uphungu ndi mphamvu ya kunkhondo. Tsono ukhulupirira yani, kuti undipandukira? Taona tsono ukhulupirira ndodo ya bango ili lothyoka, ndilo Ejipito; ndilo munthu akatsamirapo lidzamlowa m'dzanja lake ndi kuliboola; atero Farao mfumu ya Aejipito kwa onse omkhulupirira iye. Ndipo mukati kwa ine, Tikhulupirira Yehova Mulungu wathu; sindiye amene Hezekiya wamchotsera misanje yake ndi maguwa a nsembe ake, nati kwa Yuda ndi kwa Yerusalemu, Muzilambira pa guwa la nsembe pano m'Yerusalemu? Mukokerane tsono ndi mbuye wanga mfumu ya Asiriya, ndipo ndidzakupatsani akavalo zikwi ziwiri, mukakhoza inu kuonetsa apakavalo. Posakhoza kutero, mudzabweza bwanji nkhope ya nduna imodzi ya anyamata ang'ono a mbuye wanga, ndi kukhulupirira Ejipito akupatse magaleta ndi apakavalo? Ngati ndakwerera malo ano wopanda Yehova, kuwaononga? Yehova anati kwa ine, Kwerera dziko ili ndi kuliononga. Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya, ndi Sebina, ndi Yowa, anati kwa kazembeyo, Mulankhule ndi anyamata anu m'Chiaramu; popeza tichimva ichi; musalankhule nafe m'Chiyuda, chomveka ndi anthu okhala palinga. Koma kazembeyo ananena nao, Ngati mbuyanga ananditumiza kwa mbuyako, ndi kwa iwe, kunena mau awa? Si kwa anthu awa nanga okhala palinga, kuti akadye zonyansa zao, ndi kumwa mkodzo wao pamodzi ndi inu? Naima kazembeyo, nafuula ndi mau akulu m'Chiyuda, nanena kuti, Tamverani mau a mfumu yaikulu mfumu ya Asiriya. Itero mfumu, Asakunyengeni Hezekiya; pakuti sadzakhoza kukulanditsani m'dzanja lake; kapena Hezekiya asakukhulupiritseni pa Yehova, ndi kuti Yehova adzatilanditsa ndithu, ndi mudzi uwu sudzaperekedwa m'dzanja la mfumu ya Asiriya. Musamvere Hezekiya; pakuti itero mfumu ya Asiriya, Mupangane nane zamtendere, nimutulukire kwa ine, ndi kumadya yense ku mpesa wake, ndi yense ku mkuyu wake, ndi kumwa yense madzi a m'chitsime chake; mpaka ndifika ndi kumuka nanu ku dziko lakunga dziko lanu, dziko la tirigu ndi vinyo, dziko la mkate ndi minda yampesa, dziko la azitona ndi la uchi; kuti mukhale ndi moyo osafai; nimusamvere Hezekiya akakukopani, ndi kuti, Yehova adzatilanditsa. Kodi mulungu uliwonse wa amitundu walanditsa dziko lake m'dzanja la mfumu ya Asiriya ndi kale lonse? Ili kuti milungu ya Hamati, ndi ya Aripadi? Ili kuti milungu ya Sefaravaimu, kapena Hena, ndi Iva? Kodi yalanditsa Samariya m'dzanja langa? Ndi yiti mwa milungu yonse ya maiko inalanditsa maiko ao m'dzanja langa, kuti Yehova adzalanditsa Yerusalemu m'dzanja langa? Koma anthuwo anakhala chete osamyankha mau; pakuti lamulo la mfumu ndilo kuti, Musamuyankha. Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyang'anira nyumba, ndi Sebina mlembi, ndi Yowa mwana wa Asafu wolembera mbiri, anadza kwa Hezekiya ndi zovala zao zong'ambika, namuuza mau a kazembeyo. Ndipo kunali, atamva mfumu Hezekiya, anang'amba zovala zake, nafundira chiguduli, nalowa m'nyumba ya Yehova. Natuma Eliyakimu woyang'anira nyumbayo, ndi Sebina mlembi, ndi akulu a ansembe ofundira chiguduli, kwa Yesaya mneneri mwana wa Amozi. Nati kwa iye, Atero Hezekiya, Lero lino ndilo tsiku la chisautso, ndi la kudzudzula, ndi la kunyoza; pakuti ana anafikira kubadwa, koma palibe mphamvu yakubala. Kapena Yehova Mulungu wanu adzamva mau onse a kazembeyo, amene anamtuma mfumu ya Asiriya mbuye wake, kuti atonze Mulungu wamoyo, nadzamlanga chifukwa cha mau adawamva Yehova Mulungu wanu; chifukwa chake uwakwezere otsalawo pemphero. Ndipo anyamata a mfumu Hezekiya anafika kwa Yesaya. Nanena nao Yesaya, Muzitero kwa mbuye wanu, Atero Yehova, Musamaopa mau mudawamva, amene anyamata a mfumu ya Asiriya anandichitira nao mwano. Taonani, ndidzalonga mwa iye mzimu wakuti adzamva mbiri, nadzabwerera kunka ku dziko lake, ndipo ndidzamgwetsa ndi lupanga m'dziko lake. Nabwerera kazembeyo, napeza mfumu ya Asiriya alikuthira nkhondo pa Libina, popeza anamva kuti adachoka ku Lakisi. Ndipo anamva za Tirihaka mfumu ya Kusi, akuti, Taonani, watuluka kuthirana nawe nkhondo. Pamenepo anatumizanso mithenga kwa Hezekiya, ndi kuti, Muzitero naye Hezekiya mfumu ya Yuda, kuti, Asakunyenge Mulungu wako amene umkhulupirira, ndi kuti, Yerusalemu sudzaperekedwa m'dzanja la mfumu ya Asiriya. Taona, udamva icho mafumu a Asiriya anachitira maiko onse, ndi kuwaononga konse; ndipo uti upulumuke ndiwe kodi? Kodi milungu ya amitundu inawalanditsa amene makolo anga anawaononga, ndiwo Gozani, ndi Harani Rezefe, ndi ana a Edeni okhala m'Telasara? Ili kuti mfumu ya Hamati, ndi mfumu ya Aripadi, ndi mfumu ya mudzi wa Sefaravaimu, wa Hena, ndi Iva? Ndipo Hezekiya analandira kalatayo ku dzanja la mithenga, namwerenga, nakwera Hezekiya kunka kunyumba ya Yehova, namfunyulula pamaso pa Yehova. Napemphera Hezekiya pamaso pa Yehova, nati, Yehova Mulungu wa Israele wakukhala pakati pa akerubi, Inu ndinu Mulungu mwini wake, Inu nokha, wa maufumu onse a dziko lapansi; munalenga kumwamba ndi dziko lapansi. Tcherani khutu lanu, Yehova nimumve; tsegulani maso anu, Yehova, nimupenye; ndipo imvani mau a Senakeribu, amene anatumiza kutonza nao Mulungu wamoyo. Zoona, Yehova, mafumu a Asiriya anapasula amitundu ndi maiko ao, naponya milungu yao kumoto; popeza sindiyo milungu koma yopanga anthu ndi manja ao, mtengo ndi mwala; chifukwa chake anaiononga. Ndipo tsono, Yehova Mulungu wathu, mutipulumutse m'dzanja lake, kuti adziwe maufumu onse a dziko lapansi kuti Inu ndinu Yehova Mulungu, Inu nokhanokha. Pamenepo Yesaya mwana wa Amozi anatumiza kwa Hezekiya, ndi kuti, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Chondipempha iwe pa Senakeribu mfumu ya Asiriya ndachimva. Mau a Yehova akumnenera iye ndi awa, Namwali mwana wamkazi wa Ziyoni akunyoza, akuseka mwana wamkazi wa Yerusalemu, akupukusira mutu pambuyo pako. Ndiye yani wamtonza ndi kumchitira mwano? Ndiye yani wamkwezera mau ndi kumgadamira maso ako m'mwamba? Ndiye Woyerayo wa Israele. Watonza Yehova mwa mithenga yako, nuti, Ndi magaleta anga aunyinji ndakwera pa misanje ya mapiri ku mbali zake za Lebanoni, ndipo ndidzagwetsa mikungudza yake yaitali, ndi mitengo yake yosankhika yamlombwa, ndidzalowanso m'ngaka mwake mwenimweni, ku nkhalango zake za madimba. Ndakapa, ndamwa madzi achilendo, ndi ku mapazi anga ndidzaphwetsa mitsinje yonse ya Ejipito. Sunamva kodi kuti Ine ndinachichita kale lomwe, ndi kuchipanga masiku akalekale? Tsopano ndachifikitsa kuli iwe, uzikhala wakupasula midzi yamalinga ikhale miunda ya mabwinja. Chifukwa chake okhalamo ao anali ofooka manja, anaopsedwa, nachita manyazi, ananga udzu wa kuthengo, ndi msipu wauwisi, ndi udzu wa patsindwi, ndi tirigu wopserera asanakule. Koma ndidziwa kukhala pansi kwako, ndi kutuluka kwako, ndi kulowa kwako, ndi kundizazira kwako. Chifukwa cha kundizazira kwako, ndi popeza kudzikuza kwako kwandifikira m'makutu mwanga, ndidzakukowa ndi ngowe yanga m'mphuno mwako, ndi cham'kamwa changa m'milomo mwako; ndipo ndidzakubwezera pa njira unadzerayi. Ndi ichi ndi chizindikiro chako: chaka chino mudzadya za mphulumukwa, ndi chaka cha mawa za mankhokwe, ndi chaka chamkucha muzibzala ndi kukolola, muzioka minda yampesa ndi kudya zipatso zake. Ndipo opulumuka a nyumba ya Yuda otsalawo adzaphukanso mizu, ndi kupatsa zipatso pamwamba. Pakuti ku Yerusalemu kudzatuluka otsala, ndi akupulumukawo kuphiri la Ziyoni; changu cha Yehova wa makamu chidzachita ichi. Chifukwa chake atero Yehova za mfumu ya Asiriya, Iye sadzalowa m'mudzi muno, kapena kuponyamo muvi, kapena kufikako ndi chikopa, kapena kuundira mtumbira. Adzabwerera njira yomweyo anadzera, ndipo sadzalowa m'mudzi muno, ati Yehova. Pakuti ndidzatchinjiriza mudzi uno kuupulumutsa, chifukwa cha Ine mwini, ndi chifukwa cha Davide mtumiki wanga. Ndipo kunali, usiku womwewo mthenga wa Yehova anatuluka, nakantha m'misasa ya Aasiriya zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu kudza zisanu, ndipo pouka anthu mamawa, taonani, onsewo ndi mitembo. Nachoka Senakeribu mfumu ya Asiriya, namuka, nabwerera, nakhala ku Ninive. Ndipo kunali popembedza iye m'nyumba ya Nisiroki mulungu wake, Adrameleki ndi Sarezere anamkantha ndi lupanga; napulumukira ku dziko la Ararati. Ndipo Esarahadoni mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake. Masiku ajawo Hezekiya anadwala, nafuna kufa. Namdzera Yesaya mneneri mwana wa Amozi, nanena naye, Atero Yehova, Siyira banja lako; pakuti udzafa, sudzakhala ndi moyo. Pamenepo anatembenuzira nkhope yake kukhoma, napemphera kwa Yehova, ndi kuti, Mukumbukire Yehova kuti ndinayendabe pamaso panu m'choonadi, ndi mtima wangwiro, ndi kuchita zokoma m'kuona kwanu. Nalira Hezekiya kulira kwakukulu. Ndipo kunali, asanatulukire Yesaya m'kati mwa mudzi, anamdzera mau a Yehova, ndi kuti, Bwerera, nunene kwa Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga, Atero Yehova Mulungu wa Davide kholo lako, Ndamva pemphero lako, ndapenya misozi yako; taona, ndidzakuchiritsa, tsiku lachitatu udzakwera kunka kunyumba ya Yehova. Ndipo ndakuonjezera pa masiku ako zaka khumi ndi zisanu; ndidzakupulumutsa iwe ndi mudzi uno m'dzanja la mfumu ya Asiriya; ndidzatchinjiriza mudzi uno, chifukwa cha Ine ndekha, ndi chifukwa cha Davide mtumiki wanga. Nati Yesaya, Tenga nchinchi yankhuyu. Naitenga, naiika pafundo, nachira iye. Nati Hezekiya kwa Yesaya, Chizindikiro chake nchiyani kuti Yehova adzandichiza, ndi kuti ndidzakwera kunka kunyumba ya Yehova tsiku lachitatu? Nati Yesaya, Chizindikiro ndichi akupatsa Yehova, kuti Yehova adzachichita chonena Iye; kodi mthunzi umuke m'tsogolo makwerero khumi, kapena ubwerere m'mbuyo makwerero khumi? Nati Hezekiya, Kutsikira mthunzi makwerero khumi nkopepuka, kutero ai; koma mthunzi ubwerere makwerero khumi. Nafuulira kwa Yehova Yesaya mneneriyo, nabweza Iye mthunzi m'mbuyo makwerero khumi, ndiwo amene udatsikira pa makwerero a Ahazi. Nthawi ija Merodaki-Baladani mwana wa Baladani mfumu ya Babiloni anatumiza akalata ndi mtulo kwa Hezekiya, popeza adamva kuti adadwala Hezekiya. Ndipo Hezekiya anawamvera, nawaonetsa nyumba yonse ya chuma chake, siliva, ndi golide, ndi zonunkhira, ndi mafuta okometsetsa, ndi nyumba ya zida zake, ndi zonse zopezeka pachuma pake; panalibe kanthu m'nyumba mwake, kapena m'ufumu wake wonse osawaonetsa Hezekiya. Koma Yesaya mneneri anadza kwa mfumu Hezekiya, nati kwa iye, Anatani anthu awa? Anadza kwa inu kufumira kuti? Nati Hezekiya, Afumira dziko la kutali ku Babiloni. Nati iye, Anaona chiyani m'nyumba mwanu? Nati Hezekiya, Zonse za m'nyumba mwanga anaziona, palibe kanthu pachuma changa kosawaonetsa. Ndipo Yesaya anati kwa Hezekiya, Tamverani mau a Yehova. Taonani, akudza masiku kuti zonse za m'nyumba mwako, ndi zokundika makolo ako mpaka lero, zidzatengedwa kunka ku Babiloni, kosasiyidwa kanthu konse, ati Yehova. Nadzatenga ena a ana ako otuluka mwa iwe, amene udzawabala, nadzakhala iwo adindo m'chinyumba cha mfumu ya Babiloni. Pamenepo Hezekiya anati kwa Yesaya, Mau a Yehova udawanena ndi abwino. Natinso, Si momwemo nanga, mtendere ndi choonadi zikakhala masiku anga? Machitidwe ena tsono a Hezekiya, ndi mphamvu yake yonse, ndi umo anamangira dziwe ndi mchera, nautengera mudzi madzi, sizilembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda? Nagona Hezekiya ndi makolo ake; nakhala mfumu m'malo mwake Manase mwana wake. Manase anali wa zaka khumi ndi ziwiri polowa iye ufumu wake, nakhala mfumu zaka makumi asanu ndi zisanu m'Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Hepeziba. Ndipo anachita choipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonyansa za amitundu amene Yehova anawaingitsa pamaso pa ana a Israele. Pakuti anamanganso misanje, imene Hezekiya atate wake adaiononga; nautsira Baala maguwa a nsembe, nasema chifanizo, monga anachita Ahabu mfumu ya Israele, nagwadira khamu lonse la kuthambo, nalitumikira. Namanga iye maguwa a nsembe m'nyumba ya Yehova imene Yehova adainenera kuti, M'Yerusalemu ndidzaika dzina langa. Nalimangira khamu lonse la kuthambo maguwa a nsembe m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehova. Napititsa mwana wake pamoto, naombeza maula, nachita zanyanga, naika obwebweta ndi openda; anachita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wake. Ndipo anaika chifanizo chosema chimene adachipanga m'nyumba ija Yehova adainenera kwa Davide ndi kwa Solomoni mwana wake kuti, M'nyumba muno ndi m'Yerusalemu umene ndausankha mwa mafuko onse a Israele ndidzaikamo dzina langa kosatha. Ndipo sindidzachotsanso mapazi a Israele m'dziko ndidalipereka kwa makolo ao; chokhachi asamalire kuchita monga mwa zonse ndawalamulira ndi monga mwa chilamulo chonse anawalamulira Mose mtumiki wanga. Koma sanamvere, nawalakwitsa Manase, nawachititsa choipa, kuposa amitundu amene Yehova adawaononga pamaso pa ana a Israele. Pamenepo Yehova ananena mwa atumiki ake aneneri, ndi kuti, Popeza Manase mfumu ya Yuda anachita zonyansa izi, pakuti zoipa zake zinaposa zonse adazichita Aamori, amene analipo asanabadwe iye, nalakwitsanso Yuda ndi mafano ake; chifukwa chake atero Yehova Mulungu wa Israele, Taonani, nditengera Yerusalemu ndi Yuda choipa, chakuti yense achimvera chidzamliritsa mwini khutu. Ndipo ndidzayesa pa Yerusalemu chingwe choongolera cha Samariya, ndi chingwe cholungamitsira chilili cha nyumba ya Ahabu; ndidzapukuta Yerusalemu monga umo apukutira mbale, kuipukuta ndi kuivundikira. Ndipo ndidzataya chotsala cha cholowa changa, ndi kuwapereka m'dzanja la adani ao, nadzakhala iwo chakudya ndi chofunkha cha adani ao onse; popeza anachita choipa pamaso panga, nautsa mkwiyo wanga chitulukire makolo ao m'Ejipito, mpaka lero lino. Ndiponso Manase anakhetsa mwazi wambiri wosachimwa mpaka anadzaza m'Yerusalemu monsemo, osawerenga kulakwa kwake analakwitsa nako Yuda, ndi kuchita choipa pamaso pa Yehova. Machitidwe ena tsono a Manase, ndi zochimwa zonse anazichita, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda? Nagona Manase ndi makolo ake, naikidwa m'munda wa nyumba yake, m'munda wa Uza, nakhala mfumu m'malo mwake Amoni mwana wake. Amoni anali wa zaka makumi awiri mphambu ziwiri polowa iye ufumu wake, nakhala mfumu zaka ziwiri m'Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Mesulemeti mwana wa Haruzi wa ku Yotiba. Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga umo amachitira Manase atate wake. Nayenda iye m'njira monse anayendamo atate wake, natumikira mafano anawatumikira atate wake, nawagwadira; nasiya Yehova Mulungu wa makolo ake, sanayende m'njira ya Yehova. Ndipo anyamata ake a Amoni anamchitira chiwembu, napha mfumuyo m'nyumba yakeyake. Koma anthu a m'dzikomo anapha onse akumchitira chiwembu mfumu Amoni; ndipo anthu a m'dzikomo anamlonga ufumu Yosiya mwana wake m'malo mwake. Machitidwe ena tsono a Amoni adawachita, sanalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda? Naikidwa iye m'manda mwake m'munda wa Uza; nakhala mfumu m'malo mwake Yosiya mwana wake. Yosiya ndiye wa zaka zisanu ndi zitatu polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka makumi atatu mphambu chimodzi m'Yerusalemu; ndi dzina la make ndi Yedida mwana wa Adaya wa ku Bozikati. Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, nayenda m'njira yonse ya Davide kholo lake, osapatukira ku dzanja lamanja kapena kulamanzere. Ndipo kunali chaka chakhumi mphambu zisanu ndi zitatu cha Yosiya, mfumuyi inatuma Safani mwana wa Azaliya mwana wa Mesulamu, mlembi, kunyumba ya Yehova, ndi kuti, Kwera kwa Hilikiya mkulu wa ansembe, awerenge ndalama zimene anthu anabwera nazo kunyumba ya Yehova, ndizo zimene olindira pakhomo anasonkhetsa anthu; azipereke m'dzanja la antchito akuyang'anira nyumba ya Yehova; iwo azipereke kwa ogwira ntchito ya m'nyumba ya Yehova, akonze mogamuka nyumbayi, kwa amisiri a mitengo, ndi omanga nyumba, ndi omanga linga; ndi kuti agule mitengo ndi miyala yosema kukonza nazo nyumbayi. Koma sanawawerengere ndalamazo zoperekedwa m'dzanja lao, pakuti anachita mokhulupirika. Ndipo Hilikiya mkulu wa ansembe anati kwa Safani mlembi, Ndapeza buku la chilamulo m'nyumba ya Yehova. Napereka Hilikiya bukulo kwa Safani, iye naliwerenga. Ndipo Safani mlembiyo anadza kwa mfumu, nambwezera mfumu mau, nati, Anyamata anu anakhuthula ndalama zopereka m'nyumba, nazipereka m'dzanja la antchito akuyang'anira nyumba ya Yehova. Ndipo Safani mlembiyo anafotokozera mfumu, ndi kuti, Hilikiya wansembe wandipatsa buku. Nawerengamo Safani pamaso pa mfumu. Ndipo kunali, atamva mfumu mau a m'buku la chilamulo, inang'amba zovala zake. Ndipo mfumu inalamulira Hilikiya wansembe, ndi Ahikamu mwana wa Safani, ndi Akibori mwana wa Mikaya, ndi Safani mlembi, ndi Asaya mnyamata wa mfumu, ndi kuti, Mukani, funsirani ine, ndi anthu, ndi Yuda yense, kwa Yehova za mau a buku ili adalipeza; pakuti mkwiyo wa Yehova wotiyakira ife ndi waukulu; popeza atate athu sanamvere mau a buku ili, kuchita monga mwa zonse zotilemberamo. Namuka Hilikiya wansembe, ndi Ahikamu, ndi Akibori, ndi Safani, ndi Asaya, kwa Hulida mneneri wamkazi, ndiye mkazi wa Salumu mwana wa Tikiva, mwana wa Harihasi, wosunga zovala za mfumu; analikukhala iye m'Yerusalemu m'dera lachiwiri, nalankhula naye. Ndipo Hulida ananena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Muuze munthuyo anakutumizani kwa ine, Atero Yehova, Taonani, nditengera malo ano choipa, ndi iwo okhalamo, chokwaniritsa mau onse a m'buku adaliwerenga mfumu ya Yuda; popeza anandisiya Ine, nafukizira zonunkhira milungu ina, kuti autse mkwiyo wanga ndi ntchito zonse za manja ao; chifukwa chake mkwiyo wanga udzayakira malo ano wosazimikanso. Koma kwa mfumu ya Yuda amene anakutumizani kufunsira kwa Yehova, muzitero naye, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Kunena za mau udawamva, popeza mtima wako ngoolowa, ndipo unadzichepetsa pamaso pa Yehova muja udamva zonenera Ine malo ano ndi anthu okhalamo, kuti adzakhala abwinja, ndi temberero; ndipo unang'amba zovala zako ndi kulira misozi pamaso panga, Inenso ndakumvera, ati Yehova. Chifukwa chake, taona, ndidzakusonkhanitsa ukhale ndi makolo ako, nudzatengedwa ulowe m'manda mwako mumtendere; ndipo sudzaona m'maso mwako choipa chonse ndidzachifikitsira malo ano. Ndipo anambwezera mfumu mau. Pamenepo mfumu inatumiza anthu, namsonkhanitsira akulu onse a Yuda ndi a m'Yerusalemu. Nikwera mfumu kunka kunyumba ya Yehova, ndi amuna onse a Yuda, ndi onse okhala m'Yerusalemu pamodzi naye, ndi ansembe, ndi aneneri, ndi anthu onse ang'ono ndi akulu; nawerenga iye m'makutu mwao mau onse a m'buku la chipangano adalipeza m'nyumba ya Yehova. Niima mfumu pachiunda, nichita pangano pamaso pa Yehova, kutsata Yehova ndi kusunga malamulo ake, ndi mboni zake, ndi malemba ake, ndi mtima wonse ndi moyo wonse, kukhazikitsa mau a chipangano cholembedwa m'buku ili; ndipo anthu onse anaimiririra panganoli. Ndipo mfumu inalamulira Hilikiya mkulu wa ansembe, ndi ansembe a gawo lachiwiri, ndi olindira pakhomo, atulutse m'Kachisi wa Yehova zipangizo adazipangira Baala, ndi chifanizo adazipangira Baala, ndi chifanizo chija, ndi khamu lonse la kuthambo; nazitentha kunja kwa Yerusalemu ku thengo la ku Kidroni, natenga phulusa lake kunka nalo ku Betele. Naletsa ansembe opembedza mafano, amene mafumu a Yuda anawaika afukize zonunkhira pa misanje m'midzi ya Yuda, ndi pamalo pozinga Yerusalemu; iwo omwe ofukizira zonunkhira Baala, ndi dzuwa, ndi mwezi, ndi nthanda, ndi khamu lonse la kuthambo. Natulutsa chifanizocho m'nyumba ya Yehova kunja kwa Yerusalemu ku mtsinje wa Kidroni; nachitenthera ku mtsinje wa Kidroni, nachipera chikhale fumbi, naliwaza fumbi lake pa manda a ana a anthu. Nagamula nyumba za anyamata adama okhala kunyumba ya Yehova, kumene akazi anaomba nsalu zolenjeka za chifanizocho. Natulutsa ansembe onse m'midzi ya Yuda, nawaipitsira misanje, imene ansembe adafukizapo zonunkhira, kuyambira Geba kufikira Beereseba; napasula misanje ya kuzipata, yokhala polowera pa chipata cha Yoswa kazembe wa mudzi, yokhala ku dzanja lako lamanzere kwa chipata cha mudzi. Koma ansembe a misanje sanakwere kudza ku guwa la nsembe la Yehova ku Yerusalemu; koma anadya mkate wopanda chotupitsa pakati pa abale ao. Anawaipitsiranso Tofeti, wokhala m'chigwa cha ana a Hinomu; kuti asapitirize mmodzi yense mwana wake wamwamuna kapena wamkazi pamoto kwa Moleki. Nachotsanso akavalo amene mafumu a Yuda adapereka kwa dzuwa, polowera nyumba ya Yehova, ku chipinda cha Natani-Meleki mdindoyo, chokhala kukhonde; natentha magaleta a dzuwa ndi moto. Ndi maguwa a nsembe anali patsindwi pa chipinda chosanja cha Ahazi adawapanga mafumu a Yuda, ndi maguwa a nsembe adawapanga Manase m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehova, mfumu inawagumula, niwachotsa komweko, nitaya fumbi lao ku mtsinje wa Kidroni. Ndipo mfumu inawaipitsira misanje yokhala kum'mawa kwa Yerusalemu, ndiyo ya ku dzanja lamanja la phiri la chionongeko, imene Solomoni mfumu ya Israele adaimangira Asitoreti chonyansa cha Asidoni, ndi Kemosi chonyansa cha Mowabu, ndi Milikomu chonyansa cha ana a Amoni. Nathyolathyola zoimiritsa, nalikha zifanizo, nadzaza pamalo pao ndi mafupa a anthu. Anagumulanso guwa la nsembe linali ku Betele, ndi msanje adaumanga Yerobowamu mwana wa Nebati wolakwitsa Israele uja; guwa la nsembelo, ndi msanje womwe anagumula; natentha msanje, naupondereza ukhale fumbi, natentha chifanizo. Ndipo potembenuka Yosiya anaona manda okhalako kuphiri, natumiza anthu natulutsa mafupa kumanda, nawatentha pa guwa la nsembe, kuliipitsa, monga mwa mau a Yehova anawalalikira munthu wa Mulungu wolalikira izi. Anatinso, Chizindikiro ichi ndichiona nchiyani? Namuuza anthu a m'mudziwo, Ndicho manda a munthu wa Mulungu anafuma ku Yuda, nalalikira izi mwazichitira guwa la nsembe la ku Betele. Nati iye, Mlekeni, munthu asakhudze mafupa ake. Naleka iwo mafupa ake akhale pamodzi ndi mafupa a mneneri uja anatuluka m'Samariya. Ndi nyumba zonse zomwe za ku misanje yokhala m'midzi ya Samariya, adazimanga mafumu a Israele kuutsa nazo mkwiyo wa Yehova, Yosiya anazichotsa, nazichitira monga mwa ntchito zonse adazichita ku Betele. Ndipo anapha ansembe onse a misanje okhalako pa maguwa a nsembe, natentha mafupa a anthu pamenepo, nabwerera kunka ku Yerusalemu. Ndipo mfumu inalamulira anthu onse, kuti, Mchitireni Yehova Mulungu wanu Paska, monga mulembedwa m'buku ili la chipangano. Zedi silinachitika Paska lotere chiyambire masiku a oweruza anaweruza Israele, ngakhale m'masiku a mafumu a Israele, kapena mafumu a Yuda; koma Paska ili analichitira Yehova m'Yerusalemu, Yosiya atakhala mfumu zaka khumi mphambu zisanu ndi zitatu. Ndiponso obwebweta, ndi openda, ndi aterafi, ndi mafano, ndi zonyansa zonse zidaoneka m'dziko la Yuda ndi m'Yerusalemu, Yosiya anazichotsa; kuti alimbitse mau a chilamulo olembedwa m'buku adalipeza Hilikiya wansembe m'nyumba ya Yehova. Ndipo asanabadwe iye panalibe mfumu wolingana naye, imene inatembenukira kwa Yehova ndi mtima wake wonse, ndi moyo wake wonse, ndi mphamvu yake yonse, monga mwa chilamulo chonse cha Mose; atafa iyeyu sanaukenso wina wolingana naye. Koma Yehova sanakhululuke mkwiyo wake waukulu waukali umene adapsa mtima nao pa Yuda, chifukwa cha zoputa zonse Manase adaputa nazo mkwiyo wake. Nati Yehova, Ndidzachotsa Yudanso pamaso panga, monga umo ndinachotsera Israele; ndipo ndidzataya mudzi uwu ndidausankha, ndiwo Yerusalemu, ndi nyumba ndidainena, Dzina langa lidzakhala komweko. Machitidwe ena tsono a Yosiya, ndi zonse anazichita, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda? Masiku ake Farao Neko mfumu ya Aejipito anakwerera mfumu ya Asiriya ku mtsinje wa Yufurate; ndipo mfumu Yosiya anatuluka kuponyana naye, koma anapha Yosiya ku Megido, atamuona. Ndipo anyamata ake anamtengera wakufa m'galeta, nabwera naye ku Yerusalemu kuchokera ku Megido, namuika m'manda akeake. Ndipo anthu a m'dziko anatenga Yehowahazi mwana wa Yosiya, namdzoza, namlonga ufumu m'malo mwa atate wake. Yehowahazi anali wa zaka makumi awiri mphambu zitatu polowa ufumu wake, nakhala mfumu miyezi itatu m'Yerusalemu ndi dzina la make ndiye Hamutala mwana wa Yeremiya wa ku Libina. Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga umo monse adachita makolo ake. Ndipo Farao Neko anammanga m'Ribula, m'dziko la Hamati; kuti asachite ufumu m'Yerusalemu; nasonkhetsa dzikoli msonkho wa matalente zana limodzi la siliva, ndi talente limodzi la golide. Ndipo Farao Neko analonga ufumu Eliyakimu mwana wa Yosiya, m'malo mwa Yosiya atate wake, nasanduliza dzina lake likhale Yehoyakimu; koma anapita naye Yehowahazi, nafika iye m'Ejipito, nafa komweko. Ndipo Yehoyakimu anapereka siliva ndi golide kwa Farao, koma anasonkhetsa dzikoli lipereke ndalamazi; monga mwa lamulo la Farao anasonkhetsa anthu a m'dziko siliva ndi golide, yense monga mwa kuyesedwa kwake, kuzipereka kwa Farao Neko. Yehoyakimu anali wa zaka makumi awiri ndi zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi ndi chimodzi m'Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Zebida mwana wa Pedaya wa Ruma. Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazichita makolo ake. Masiku ake Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anakwerako, Yehoyakimu nagwira mwendo wake zaka zitatu; pamenepo anatembenuka nampandukira. Ndipo Yehova anamtumizira magulu a Ababiloni, ndi magulu a Aaramu, ndi magulu a Amowabu, ndi magulu a ana a Amoni, nawatumiza pa Yuda kuliononga, monga mwa mau a Yehova adawanena ndi dzanja la atumiki ake aneneriwo. Zedi ichi chinadzera Yuda mwa lamulo la Yehova, kuwachotsa pamaso pake, chifukwa cha zolakwa za Manase, monga mwa zonse anazichita; ndiponso chifukwa cha mwazi wosachimwa adaukhetsa; popeza anadzaza Yerusalemu ndi mwazi wosachimwa; ndipo Yehova sanafune kukhululukira. Machitidwe ena tsono a Yehoyakimu, ndi zonse anazichita, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda? Nagona Yehoyakimu ndi makolo ake, ndipo Yehoyakini mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake. Koma mfumu ya Aejipito sinabwerezanso kutuluka m'dziko lake, pakuti mfumu ya Babiloni idalanda kuyambira ku mtsinje wa Ejipito kufikira ku mtsinje Yufurate, ndilo lonse anali nalo mfumu ya Aejipito. Yehoyakini anali wa zaka khumi mphambu zisanu ndi zitatu polowa iye ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu miyezi itatu; ndi dzina la make ndiye Nehusita mwana wa Elinatani wa ku Yerusalemu. Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga umo monse adachita atate wake. Nthawi ija anyamata a Nebukadinezara mfumu ya Babiloni anakwerera Yerusalemu, naumangira mudziwo misasa. Nafika Nebukadinezara mfumu ya Babiloni kumudzi, ataumangira misasa anyamata ake, Ndipo Yehoyakini mfumu ya Yuda anatulukira kwa mfumu ya Babiloni, iye ndi make, ndi anyamata ake, ndi akalonga ake, ndi adindo ake; mfumu ya Babiloni nimtenga chaka chachisanu ndi chitatu cha ufumu wake. Natulutsa kuchotsa komweko chuma chonse cha nyumba ya Yehova, ndi chuma cha nyumba ya mfumu, naduladula zipangizo zonse zagolide adazipanga Solomoni mfumu ya Israele m'Kachisi wa Yehova, monga Yehova adanena. Nachoka nao a m'Yerusalemu onse, ndi akalonga onse, ndi ngwazi zonse, ndiwo andende zikwi khumi, ndi amisiri onse, ndi osula onse; sanatsale ndi mmodzi yense, koma anthu osauka okhaokha a m'dziko. Nachoka naye Yehoyakini kunka naye ku Babiloni, ndi make wa mfumu, ndi akazi a mfumu, ndi adindo ake, ndi omveka a m'dziko; anachoka nao andende ku Yerusalemu kunka nao ku Babiloni. Ndi anthu amphamvu onse, ndiwo zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi amisiri, ndi osula chikwi chimodzi, onsewo achamuna oyenera nkhondo, omwewo mfumu ya Babiloni anadza nao andende ku Babiloni. Ndipo mfumu ya Babiloni analonga Mataniya mbale wa atate wake akhale mfumu m'malo mwake, nasanduliza dzina lake likhale Zedekiya. Zedekiya anali wa zaka makumi awiri mphambu chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi ndi chimodzi m'Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Hamutala mwana wa Yeremiya wa ku Libina. Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adachita Yehoyakimu. Pakuti mwa mkwiyo wa Yehova zonse zidachitika m'Yerusalemu ndi m'Yuda, mpaka adawataya pamaso pake; ndipo Zedekiya anapandukira mfumu ya Babiloni. Ndipo kunali chaka chachisanu ndi chinai cha ufumu wake, mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya Babiloni, iye ndi khamu lake lonse anadzera Yerusalemu, naumangira misasa, naumangira timalinga mouzinga. Ndipo mudziwo unazingidwa ndi timalinga mpaka chaka chakhumi ndi chimodzi cha mfumu Zedekiya. Tsiku lachisanu ndi chinai la mwezi wachinai njala idakula m'mudzimo, panalibe chakudya kwa anthu a m'dzikomo. Pamenepo linga la mudziwo linagamulidwa, nathawira ankhondo onse usiku, njira ya ku chipata cha pakati pa makoma awiri, ili ku munda wa mfumu; Ababiloni tsono anali pamudzi pouzinga; nimuka mfumu pa njira ya kuchidikha. Koma nkhondo ya Ababiloni inalondola mfumu, niipeza m'zidikha za Yeriko; koma nkhondo yake yonse inambalalikira. Ndipo anaigwira mfumu, nakwera nayo kwa mfumu ya Babiloni ku Ribula, naweruza mlandu wake. Napha ana a Zedekiya pamaso pake, namkolowola Zedekiya maso ake, nammanga ndi maunyolo amkuwa, namuka naye ku Babiloni. Ndipo mwezi wachisanu, tsiku lachisanu ndi chiwiri la mweziwo, ndicho chaka chakhumi mphambu chisanu ndi chinai cha mfumu Nebukadinezara mfumu ya Babiloni, Nebuzaradani mkulu wa olindirira, ndiye mnyamata wa mfumu ya Babiloni, anadza ku Yerusalemu, natentha nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi nyumba zonse za m'Yerusalemu; ndi nyumba zonse zazikulu anazitentha ndi moto. Ndi khamu lonse la Ababiloni linali ndi mkulu wa olindirira linagumula linga la Yerusalemu louzinga. Ndi anthu otsalira m'mudzi, ndi opanduka akuthawira kwa mfumu ya Babiloni, ndi aunyinji otsalira, Nebuzaradani mkulu wa olindirira anamuka nao andende. Koma mkulu wa olindirira anasiya osaukadi a m'dziko akhale osunga minda yampesa, ndi alimi. Ndipo zoimiritsa zamkuwa zinali m'nyumba ya Yehova, ndi maphaka ake, ndi thawale lamkuwa, zinali m'nyumba ya Yehova, Ababiloni anazithyolathyola, natenga mkuwa wake kunka nao ku Babiloni. Nachotsanso miphika, ndi zoolera, ndi zozimira nyali, ndi zipande, ndi zipangizo zonse zamkuwa zimene anatumikira nazo. Ndi zopalira moto, ndi mbale zowazira za golide yekhayekha, ndi zasiliva yekhayekha, mkulu wa asilikali anazichotsa. Nsanamira ziwiri, thawale limodzi, ndi maphakawo adazipangira nyumba ya Yehova Solomoni, mkuwa wa zipangizo izi zonse sanakhoze kuyesa kulemera kwake. Msinkhu wake wa nsanamira imodzi ndiwo mikono khumi mphambu isanu ndi itatu, ndi pamwamba pake mutu wamkuwa; ndi msinkhu wake wa mutuwo ndiwo mikono itatu, ndi ukonde, ndi makangaza pamutu pouzinga, zonse zamkuwa; ndi nsanamira inzake inali nazo zomwezo pamodzi ndi ukonde. Ndipo mkulu wa olindirira anatenga Seraya wansembe wamkulu, ndi Zefaniya wansembe wachiwiri, ndi olindira pakhomo atatu; natenga m'mudzimo mdindo woikidwa woyang'anira ankhondo; ndi anthu asanu a iwo openya nkhope ya mfumu opezeka m'mudzimo; ndi mlembi, kazembe wa nkhondo wolembera anthu a m'dziko; ndi anthu a m'dziko makumi asanu ndi limodzi opezeka m'mudzimo. Ndipo Nebuzaradani mkulu wa olindirira anawatenga, napita nao kwa mfumu ya Babiloni ku Ribula. Niwakantha mfumu ya Babiloni, niwaphera ku Ribula m'dziko la Hamati. Motero anamuka nao Ayuda andende kuwachotsa m'dziko lao. Koma kunena za anthu otsalira m'dziko la Yuda, amene adawasiya Nebukadinezara mfumu ya Babiloni, iyeyu anamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani akhale wowalamulira. Ndipo pamene anamva akazembe onse a makamu, iwo ndi anthu ao, kuti mfumu ya Babiloni adaika Gedaliya wowalamulira, anadza kwa Gedaliya ku Mizipa, ndiwo Ismaele mwana wa Netaniya, ndi Yohanani mwana wa Kareya, ndi Seraya mwana wa Tanumeti wa ku Netofa, ndi Yazaniya mwana wa Mmaakati, iwo ndi anthu ao omwe. Nawalumbirira Gedaliya iwo ndi anthu ao, nanena nao, Musamaopa anyamata a Ababiloni; khalani m'dziko; tumikirani mfumu ya Babiloni, ndipo kudzakukomerani. Koma kunali mwezi wachisanu ndi chiwiri anadza Ismaele mwana wa Netaniya mwana wa Elisama, wa mbumba yachifumu, ndi anthu khumi pamodzi naye, nakantha Gedaliya; nafa iye, ndi Ayuda, ndi Ababiloni okhala naye ku Mizipa. Pamenepo ananyamuka anthu onse ang'ono ndi akulu, ndi akazembe a makamu, nadza ku Ejipito; pakuti anaopa Ababiloni. Ndipo kunali chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi ziwiri cha kumtenga ndende Yehoyakini mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi ndi ziwiri, tsiku la makumi awiri mphambu asanu ndi awiri la mwezi, Evili-Merodaki mfumu ya Babiloni anamuweramutsa mutu wake wa Yehoyakini mfumu ya Yuda atuluke m'kaidi, chaka cholowa iye ufumu wake; nakamba naye zokoma, namkweza mpando wake waulemu upose mipando ya mafumu anali pamodzi naye m'Babiloni. Nasintha zovala zake za m'kaidi, namadya iye mkate pamaso pake masiku onse a moyo wake. Ndi kunena za chakudya chake, panali chakudya chosalekeza chopatsidwa kwa iye ndi mfumu, tsiku lililonse gawo lake, masiku onse a moyo wake. Adamu, Seti, Enosi, Kenani, Mahalalele, Yaredi, Enoki, Metusela, Lameki, Nowa, Semu, Hamu, ndi Yafeti. Ana a Yafeti: Gomeri, ndi Magogi, ndi Madai, ndi Yavani, ndi Tubala, ndi Meseki, ndi Tirasi. Ndi ana a Gomeri: Asikenazi, Difati, ndi Togarima. Ndi ana a Yavani: Elisa, ndi Tarisisi, Kitimu, ndi Rodanimu. Ana a Hamu: Kusi, ndi Ejipito, Puti, ndi Kanani. Ndi ana a Kusi: Seba, ndi Havila, ndi Sabita, ndi Raama, ndi Sabiteka. Ndi ana a Raama: Sheba, ndi Dedani. Ndi Kusi anabala Nimirodi; iye anayamba kukhala wamphamvu pa dziko. Ndi Ejipito anabala Aludi, ndi Aanamimu, ndi Alehabu, ndi Anafituhimu, ndi Apatirusi, ndi Akasiluhimu, (kumene anafuma Afilisti), ndi Akafitori. Ndi Kanani anabala Sidoni mwana wake woyamba, ndi Heti, ndi Ayebusi, ndi Aamori, ndi Agirigasi, ndi Ahivi, ndi Aariki, ndi Asini, ndi Aaravadi, ndi Azemari, ndi Ahamati. Ana a Semu: Elamu, ndi Asiriya, ndi Aripakisadi, ndi Ludi, ndi Aramu, ndi Uzi, ndi Huli, ndi Getere, ndi Meseki. Ndi Aripakisadi anabala Sela; ndi Sela anabala Eberi. Ndi Eberi anabala ana amuna awiri, dzina la winayo ndiye Pelegi, popeza masiku ake dziko linagawanika; ndi dzina la mbale wake ndiye Yokotani. Ndipo Yokotani anabala Alimodadi, ndi Selefi, ndi Hazara-Maveti, ndi Yera; ndi Hadoramu, ndi Uzali, ndi Dikila; ndi Ebala, ndi Abimaele, ndi Sheba, ndi Ofiri, ndi Havila, ndi Yobabu. Awa onse ndiwo ana a Yokotani. Semu, Aripakisadi, Sela; Eberi, Pelegi, Reu, Serugi, Nahori, Tera; Abramu, (ndiye Abrahamu). Ana a Abrahamu: Isaki, ndi Ismaele. Mibadwo yao ndi awa; woyamba wa Ismaele Nebayoti; ndi Kedara ndi Adibeele, ndi Mibisamu, Misima, ndi Duma, Masa, Hadadi, ndi Tema, Yeturi, Nafisi, ndi Kedema. Awa ndi ana a Ismaele. Ndi ana a Ketura mkazi wamng'ono wa Abrahamu anabala Zimirani, ndi Yokisani, ndi Medani, ndi Midiyani, ndi Isibaki, ndi Suwa. Ndi ana a Yokisani: Sheba, ndi Dedani. Ndi ana a Midiyani: Efa, ndi Efere, ndi Hanoki, ndi Abida, ndi Elida. Awa onse ndiwo ana a Ketura. Ndipo Abrahamu anabala Isaki. Ana a Isaki: Esau, ndi Israele. Ana a Esau: Elifazi, Reuwele, ndi Yeusi, ndi Yalamu, ndi Kora. Ana a Elifazi: Temani, ndi Omara, Zefi, ndi Gatamu, Kenazi, ndi Timna, ndi Amaleke. Ana a Reuwele: Nahati, Zera, Sama, ndi Miza. Ndi ana a Seiri: Lotani, ndi Sobala, ndi Zibiyoni, ndi Ana, ndi Disoni, ndi Ezere, ndi Disani. Ndi ana a Lotani: Hori, ndi Homamu; ndipo Timna ndiye mlongo wake wa Lotani. Ana a Sobala: Aliyani, ndi Manahati, ndi Ebala, Sefi, ndi Onamu. Ndi ana a Zibiyoni: Aiya ndi Ana. Mwana wa Ana: Disoni. Ndi ana a Disoni: Hamurani, ndi Esibani, ndi Itirani, ndi Kerani. Ana a Ezere: Bilihani, ndi Zaavani, ndi Yaakani. Ana a Disani: Uzi, ndi Arani. Mafumu tsono akuchita ufumu m'dziko la Edomu, pakalibe mfumu wakuchita ufumu pa ana a Israele, ndiwo Bela mwana wa Beori; ndi dzina la mudzi wake ndilo Dinihaba. Ndipo anafa Bela; ndi Yobabu mwana wa Zera wa ku Bozira anakhala mfumu m'malo mwake. Namwalira Yobabu; ndi Husamu wa ku dziko la Atemani anakhala mfumu m'malo mwake. Namwalira Husamu; ndi Hadadi mwana wa Bedadi, amene anakantha Midiyani ku thengo la Mowabu, anakhala mfumu m'malo mwake; ndi dzina la mudzi wake ndi Aviti. Namwalira Hadadi; ndi Samila wa ku Masireka anakhala mfumu m'malo mwake. Namwalira Samila: ndi Shaulo wa ku Rehoboti ku nyanja anakhala mfumu m'malo mwake. Namwalira Shaulo; ndi Baala-Hanani mwana wa Akibori anakhala mfumu m'malo mwake. Namwalira Baala-Hanani; ndi Hadadi anakhala mfumu m'malo mwake; ndipo dzina la mudzi wake ndi Pai; ndi dzina la mkazi wake ndiye Mehetabele mwana wamkazi wa Matiredi mwana wamkazi wa Mezahabu. Namwalira Hadadi. Ndipo mafumu a Edomu ndiwo mfumu Timna, mfumu Aliva, mfumu Yeteti; mfumu Oholibama, mfumu Ela, mfumu Pinoni; mfumu Kenazi, mfumu Temani, mfumu Mibizara; mfumu Magadiele, mfumu Iramu. Awa ndi mafumu a Edomu. Ana a Israele ndi awa: Rubeni, Simeoni, Levi, ndi Yuda, Isakara, ndi Zebuloni, Dani, Yosefe, ndi Benjamini, Nafutali, Gadi, ndi Asere. Ana a Yuda ndiwo Eri, ndi Onani, ndi Sela; Batisuwa Mkanani anambalira atatu amenewa. Koma Eri mwana woyamba wa Yuda anali woipa pamaso pa Yehova, ndi Iye anamupha. Ndi Tamara mpongozi wake anambalira Perezi ndi Zera. Ana amuna onse a Yuda ndiwo asanu. Ana a Perezi: Hezironi, ndi Hamuli. Ndi ana a Zera: Zimiri, ndi Etani, ndi Hemani, ndi Kalikoli, ndi Dara; onse pamodzi ndi asanu. Ndi ana a Karimi: Akara wovuta Israeleyo, amene analakwira choperekedwa chiperekerecho. Ndi mwana wa Etani: Azariya. Ndi ana a Hezironi anambadwirawo: Yerameele, ndi Ramu, ndi Kalebe. Ndi Ramu anabala Aminadabu; ndi Aminadabu anabala Nasoni kalonga wa ana a Yuda; ndi Nasoni anabala Salimoni, ndi Salimoni anabala Bowazi, ndi Bowazi anabala Obedi, ndi Obedi anabala Yese, ndi Yese anabala mwana wake wamwamuna woyamba Eliyabu, ndi Abinadabu wachiwiri, ndi Simea wachitatu, Netanele wachinai, Radai wachisanu, Ozemu wachisanu ndi chimodzi, Davide wachisanu ndi chiwiri; ndi alongo ao ndiwo Zeruya ndi Abigaile. Ndi ana a Zeruya: Abisai ndi Yowabu, ndi Asahele; atatu. Ndi Abigaile anabala Amasa; ndi atate wa Amasa ndiye Yetere Mwismaele. Ndi Kalebe mwana wa Hezironi anabala ana ndi Azuba mkazi wake, ndi Yerioti; ndipo ana ake ndiwo Yesere, ndi Sobabu, ndi Aridoni. Namwalira Azuba, ndi Kalebe anadzitengera Efurata, amene anambalira Huri. Ndi Huri anabala Uri, ndi Uri anabala Bezalele. Ndipo pambuyo pake Hezironi analowa kwa mwana wamkazi wa Makiri atate wa Giliyadi, amene anamtenga akhale mkazi wake, pokhala wa zaka makumi asanu ndi limodzi mwamunayo; ndipo mkaziyo anambalira Segubu. Ndi Segubu anabala Yairi, amene anali nayo midzi makumi awiri mphambu itatu m'dziko la Giliyadi. Ndi Gesuri ndi Aramu analanda midzi ya Yairi, pamodzi ndi Kenati ndi milaga yake; ndiyo midzi makumi asanu ndi limodzi. Iwo onse ndiwo ana a Makiri atate wa Giliyadi. Ndipo atafa Hezironi m'Kalebe-Efurata, Abiya mkazi wa Hezironi anambalira Asiriya atate wa Tekowa. Ndi ana a Yerameele mwana woyamba wa Hezironi ndiwo: woyamba Ramu, ndi Buna, ndi Oreni, ndi Ozemu, ndi Ahiya. Ndipo Yerameele anali naye mkazi wina dzina lake ndiye Atara, ndiye make wa Onamu. Ndipo ana a Ramu mwana woyamba wa Yerameele ndiwo Maazi, ndi Yamini, ndi Ekeri. Ndi ana a Onamu ndiwo Samai, ndi Yada; ndi ana a Samai: Nadabu, ndi Abisuri. Ndipo dzina la mkazi wa Abisuri ndiye Abihaili; ndipo anambalira Abani, ndi Molidi. Ndi ana a Nadabu: Seledi ndi Apaimu; koma Seledi anamwalira wopanda ana. Ndi mwana wa Apaimu: Isi. Ndi mwana wa Isi: Sesani. Ndi mwana wa Sesani: Alai. Ndi ana a Yada mbale wa Samai: Yetere, ndi Yonatani; namwalira Yetere wopanda ana. Ndi ana a Yonatani: Peleti, ndi Zaza. Ndiwo ana a Yerameele. Ndipo Sesani analibe ana amuna, koma ana akazi. Ndi Sesani anali naye mnyamata Mwejipito dzina lake ndiye Yara. Ndipo Sesani anampatsa Yara mnyamata wake mwana wake wamkazi akhale mkazi wake, ndipo anambalira Atai. Ndipo Atai anabala Natani, ndi Natani anabala Zabadi, ndi Zabadi anabala Efilala, ndi Efilala anabala Obedi, ndi Obedi anabala Yehu, ndi Yehu anabala Azariya, ndi Azariya anabala Helezi, ndi Helezi anabala Eleasa, ndi Eleasa anabala Sisimai, ndi Sisimai anabala Salumu, ndi Salumu anabala Yekamiya, ndi Yekamiya anabala Elisama. Ndi ana a Kalebe mbale wa Yerameele ndiwo Mesa mwana wake woyamba, ndiye atate wa Zifi; ndi ana a Maresa atate wa Hebroni. Ndi ana a Hebroni: Kora, ndi Tapuwa, ndi Rekemu, ndi Sema. Ndi Sema anabala Rahama atate wa Yorikeamu, ndi Rekemu anabala Samai. Ndi mwana wa Samai ndiye Maoni; ndipo Maoni ndiye atate wa Betezuri. Ndi Efa mkazi wamng'ono wa Kalebe anabala Harani, ndi Moza, ndi Gazezi; ndi Harani anabala Gazezi. Ndi ana a Yadai: Regemu, ndi Yotamu, ndi Gesani, ndi Peleti, ndi Efa, ndi Saafi. Maaka mkazi wamng'ono wa Kalebe anabala Sebere, ndi Tirihana. Iyeyu anabalanso Saafi atate wa Madimana, Seva atate wa Makibena, ndi atate wa Gibea; ndi mwana wamkazi wa Kalebe ndiye Akisa. Ana a Kalebe ndi awa: mwana wa Huri, mwana woyamba wa Efurata, Sobala atate wa Kiriyati-Yearimu. Salima atate wa Betelehemu, Harefi atate wa Betegadere. Ndipo Sobala atate wa Kiriyati-Yearimu anali ndi ana: Harowe, ndi Hazi Amenuwoti. Ndi mabanja a Kiriyati-Yearimu: Aitiri, ndi Aputi, ndi Asumati, ndi Amisrai; Azorati ndi Aestaoli anafuma kwa iwowa. Ana a Salima: Betelehemu, ndi Anetofa, Ataroti-Beti-Yowabu, ndi Hazi Amanahati, ndi Azori. Ndi mabanja a alembi okhala ku Yabezi: Atirati, Asimeati, Asukati. Iwo ndiwo Akeni ofuma ku Hamati, kholo la nyumba ya Rekabu. Ana a Davide tsono ombadwira ku Hebroni: woyamba Aminoni wa Ahinowamu wa ku Yezireele, wachiwiri Daniele wa Abigaile wa ku Karimele, wachitatu Abisalomu mwana wa Maaka mwana wamkazi wa Talimai mfumu ya Gesuri, wachinai Adoniya mwana wa Hagiti, wachisanu Sefatiya wa Abitala, wachisanu ndi chimodzi Itireamu wa mkazi wake Egila. Anambadwira asanu ndi mmodzi m'Hebroni; ndi pomwepo anakhala mfumu zaka zisanu ndi ziwiri, ndi miyezi isanu ndi iwiri; ndi m'Yerusalemu anakhala mfumu zaka makumi atatu mphambu zitatu. Ndipo ombadwira m'Yerusalemu ndi awa: Simea, ndi Sobabu, ndi Natani, ndi Solomoni, anai a Batisuwa mwana wamkazi wa Amiyele; ndi Ibara, ndi Elisama, ndi Elifeleti, ndi Noga, ndi Nefegi, ndi Yafiya, ndi Elisama, ndi Eliyada, ndi Elifeleti, asanu ndi anai. Onsewa ndiwo ana a Davide, pamodzi ndi ana a akazi aang'ono; ndipo Tamara ndiye mlongo wao. Ndipo mwana wa Solomoni ndiye Rehobowamu, Abiya mwana wake, Asa mwana wake, Yehosafati mwana wake, Yoramu mwana wake, Ahaziya mwana wake, Yowasi mwana wake, Amaziya mwana wake, Azariya mwana wake, Yotamu mwana wake, Ahazi mwana wake, Hezekiya mwana wake, Manase mwana wake, Amoni mwana wake, Yosiya mwana wake. Ndi ana a Yosiya: woyamba Yohanani, wachiwiri Yehoyakimu, wachitatu Zedekiya, wachinai Salumu. Ndi ana a Yehoyakimu: Yekoniya mwana wake, Zedekiya mwana wake. Ndi mwana wa Yekoniya: Asiri, Sealatiele mwana wake, ndi Malikiramu, ndi Pedaya, ndi Senazara, Yekamiya, Hosama, Nedabiya. Ndi ana a Pedaya: Zerubabele ndi Simei; ndi ana a Zerubabele: Mesulamu, ndi Hananiya; ndipo Selomiti ndiye mlongo wao, ndi Hasuba, ndi Ohele, ndi Berekiya, ndi Hasadiya, ndi Yusabu-hesede; asanu. Ndi ana a Hananiya: Pelatiya, ndi Yesaya, ana a Refaya, ana a Arinani, ana a Obadiya, ana a Sekaniya. Ndi mwana wa Sekaniya: Semaya; ndi ana a Semaya: Hatusi, ndi Igala, ndi Bariya, ndi Neariya, ndi Safati; asanu ndi mmodzi. Ndi ana a Neariya: Eliyoenai, ndi Hizikiya, ndi Azirikamu, atatu. Ndi ana a Eliyoenai: Hodaviya, ndi Eliyasibu, ndi Pelaya, ndi Akubu, ndi Yohanani, ndi Delaya, ndi Anani, asanu ndi awiri. Ana a Yuda: Perezi, Hezironi, ndi Karimi, ndi Huri, ndi Sobala. Ndipo Reaya mwana wa Sobala anabala Yahati; ndi Yahati anabala Ahumai, ndi Lahadi. Iwo ndiwo mabanja a Azorati. Iwo ndiwo a atate wa Etamu: Yezireele, ndi Isima, ndi Idibasi; ndipo dzina la mlongo wao ndiye Hazeleleponi, ndi Penuwele atate wa Gedori, ndi Ezere atate wa Husa. Awa ndi ana a Huri woyamba wa Efurata atate wa Betelehemu. Ndipo Asiriya atate wa Tekowa anali nao akazi awiri: Hela, ndi Naara. Ndi Naara anambalira Ahuzamu, ndi Hefere, ndi Temeni, ndi Haahasitari. Iwo ndiwo ana a Naara. Ndi ana a Hela ndiwo Zereti, Izihara, ndi Etinani. Ndipo Hakozi anabala Anubu, ndi Zobeba, ndi mabanja a Ahariyele mwana wa Harumu. Ndipo Yabezi analemekezedwa koposa abale ake; ndi make anamutcha dzina lake Yabezi, ndi kuti, Popeza ndambala mwaululu. Ndipo Yabezi anaitana kwa Mulungu wa Israele, ndi kuti, Mundidalitse ndithu, ndi kukulitsa malire anga; ndi dzanja lanu likhale ndi ine, nimundisunge, kuti choipa chisandivute. Ndipo Mulungu anafikitsa chopempha iye. Ndipo Kelubu mbale wa Suha anabala Mehiri, ndiye atate wa Esitoni. Ndi Esitoni, anabala Beterafa, ndi Paseya, ndi Tehina atate wa Irinahasi. Awa ndi anthu a Reka. Ndi ana a Kenazi: Otiniyele, ndi Seraya; ndi mwana wa Otiniyele: Hatati. Ndipo Meonotai anabala Ofura; ndi Seraya anabala Yowabu atate wa Geharasimu; popeza iwo ndiwo amisiri. Ndi ana a Kalebe mwana wa Yefune: Iru, Ela, ndi Naamu; ndi ana a Ela, ndi Kenazi. Ndi ana a Yehalelele: Zifi, ndi Zifa, Tiriya, ndi Asarele. Ndi ana a Ezara: Yetere, ndi Meredi, ndi Efere, ndi Yaloni; ndipo anabala Miriyamu, ndi Samai, ndi Isiba atate wa Esitemowa. Ndi mkazi wake Myuda anabala Yeredi atate wa Gedori, ndi Hebere atate wa Soko, ndi Yekutiyele atate wa Zanowa. Ndipo awa ndi ana a Bitiya mwana wamkazi wa Farao, amene Meredi anamtenga. Ndi ana a mkazi wa Hodiya, mlongo wake wa Nahamu, ndiwo atate a Keila Mgarimi ndi Esitemowa Mmaaka. Ndi ana a Simoni; Aminoni, ndi Rina, Benihanani, ndi Tiloni. Ndi ana a Isi: Zoheti, ndi Benizoheti. Ana a Sela mwana wa Yuda: Eri atate wa Leka, ndi Laada atate wa Maresa, ndi mabanja a nyumba ya iwo oomba bafuta wa thonje losansitsa a nyumba ya Asibeya, ndi Yokimu, ndi amuna a Kozeba, ndi Yowasi, ndi Sarafi wolamulira m'Mowabu, ndi Yasubilehemu; koma mau awa ndiwo a kale lomwe. Iwo ndiwo oumba mbiya, ndi okhala m'Netaimu, ndi m'Gedera; anakhala komweko ndi mfumu m'ntchito yake. Ana a Simeoni: Nemuwele, ndi Yamini, Yaribu, Zera, Shaulo, Salumu mwana wake, Mibisamu mwana wake, Misima mwana wake. Ndi ana a Misima: Hamuele mwana wake, Zakuri mwana wake, Simei mwana wake. Ndipo Simei anali nao ana amuna khumi mphambu asanu ndi mmodzi, ndi ana akazi asanu ndi mmodzi; koma abale ake analibe ana ambiri, ndi banja lao lonse silinachulukitsa ngati ana a Yuda. Ndipo anakhala ku Beereseba, ndi Molada, ndi Hazara-Suwala, ndi ku Biliha, ndi ku Ezemu, ndi ku Toladi, ndi ku Betuele, ndi ku Horoma, ndi ku Zikilagi, ndi ku Betemara-Kaboti, ndi ku Hazara-Susimu, ndi ku Betebiri, ndi ku Saaraimu. Iyi ndi midzi yao, mpaka ufumu wa Davide, pamodzi ndi milaga yao. Etamu, ndi Aini, Rimoni, ndi Tokeni, ndi Asani, midzi isanu; ndi milaga yao yonse pozungulira pake pa midzi yomweyi, mpaka Baala. Apo ndi pokhala pao ndipo ali nao mawerengedwe a maina ao. Ndi Mesobabu, ndi Yamuleki, ndi Yosa mwana wa Amaziya, ndi Yowele, ndi Yehu mwana wa Yosibiya, mwana wa Seraya, mwana wa Asiyele; ndi Eliyoenai, ndi Yaakoba, ndi Yesohaya, ndi Asaya, ndi Adiyele, ndi Yesimiele, ndi Benaya, ndi Ziza mwana wa Sifi, mwana wa Aloni, mwana wa Yedaya, mwana wa Simiri, mwana wa Semaya; awa otchedwa maina ndiwo akalonga m'mabanja ao, ndi nyumba za makolo ao zinachuluka kwambiri. Ndipo anamuka mpaka polowera ku Gedori kum'mawa kwa chigwa, kufunafuna podyetsa zoweta zao. Ndipo anapeza podyetsa ponenepetsa ndi pabwino, ndipo dzikoli ndi lachitando ndi lodikha ndi losungikamo, pakuti okhalako kale ndiwo a Hamu. Iwo tsono olembedwa maina anadza masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda, nakantha mahema ao ndi zokhalamo zao, naziononga konse mpaka lero, nakhala m'malo mwao; popeza panali podyetsa zoweta zao pamenepo. Ndipo ena a iwowa a ana a Simeoni, amuna mazana asanu, ananka kuphiri la Seiri; akuwatsogolera ndiwo Pelatiya, ndi Neariya, ndi Refaya, ndi Uziyele; ana a Isi. Nakantha otsala a Aamaleke adapulumukawo, nakhala komweko mpaka lero lino. Ndipo ana a Rubeni mwana woyamba wa Israele, (pakuti ndiye mwana woyamba; koma popeza anaipsa kama wa atate wake ukulu wake unapatsidwa kwa ana a Yosefe mwana wa Israele, koma m'buku la chibadwidwe asayesedwe monga mwa ukulu wake. Pakuti Yuda anakula mphamvu mwa abale ake, ndi mtsogoleri anafuma kwa iyeyu, koma ukulu ngwa Yosefe); ana a Rubeni mwana woyamba wa Israele: Hanoki, ndi Palu, Hezironi, ndi Karimi. Ana a Yowele: Semaya mwana wake, Gogi mwana wake, Simei mwana wake, Mika mwana wake, Reaya mwana wake, Baala mwana wake, Beera mwana wake, amene Tigilati-Pilesere mfumu ya ku Asiriya anamtenga ndende; ndiye kalonga wa Arubeni. Ndi abale ake monga mwa mabanja ao, powerenga chibadwidwe cha mibadwo yao: akulu ndiwo Yeiyele, ndi Zekariya, ndi Bela mwana wa Azazi, mwana wa Sema, mwana wa Yowele, wokhala ku Aroere, ndi kufikira ku Nebo ndi Baala-Meoni; ndi kum'mawa anakhala mpaka polowera kuchipululu kuyambira mtsinje wa Yufurate; pakuti zoweta zao zinachuluka m'dziko la Giliyadi. Ndipo masiku a Saulo anagwirana nkhondo ndi Ahagiri, amene adagwa ndi dzanja lao; ndipo anakhala m'mahema mwao kum'mawa konse kwa Giliyadi. Ndi ana a Gadi anakhala pandunji pao m'dziko la Basani mpaka Saleka: Yowele mkulu wao, ndi Safamu wachiwiri, ndi Yanai, ndi Safati m'Basani; ndi abale ao a nyumba za makolo ao: Mikaele, ndi Mesulamu, ndi Sheba, ndi Yorai, ndi Yakani, ndi Ziya, ndi Eberi; asanu ndi awiri. Awa ndi ana a Abihaili, mwana wa Huri, mwana wa Yarowa, mwana wa Giliyadi, mwana wa Mikaele, mwana wa Yesisai, mwana wa Yado, mwana wa Buzi, Ahi mwana wa Abidiyele, mwana wa Guni, ndiye mkulu wa nyumba za makolo ao. Ndipo anakhala m'Giliyadi m'Basani, ndi m'midzi yake, ndi podyetsa pake ponse pa Saroni, mpaka malire ao. Onsewo anawerengedwa monga mwa mabuku a chibadwidwe chao, masiku a Yotamu mfumu ya Yuda, ndi m'masiku a Yerobowamu mfumu ya Israele. Ana a Rubeni, ndi a Gadi, ndi limodzi la magawo awiri a fuko la Manase, ngwazi, amuna akugwira chikopa ndi lupanga, ndi kuponya mivi, ozolowera nkhondo, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zinai mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi limodzi akutuluka kunkhondo. Ndipo anagwirana nkhondo ndi Ahagiri, ndi Yeturi, ndi Nafisi, ndi Nodabu. Ndipo anathandizidwa polimbana nao; ndi Ahagiri anaperekedwa m'dzanja lao, ndi onse anali nao; pakuti anafuulira kwa Mulungu pomenyana nao, ndipo anapembedzeka nao, popeza anamkhulupirira Iye. Ndipo analanda zoweta zao, ngamira zao zikwi makumi asanu, ndi nkhosa zikwi mazana awiri ndi makumi asanu, ndi abulu zikwi ziwiri, ndi amuna zikwi zana limodzi. Pakuti adagwa, nafa ambiri, popeza nkhondoyi nja Mulungu. Ndipo anakhala m'malo mwao mpaka anatengedwa ndende. Ndi ana a limodzi la magawo awiri a fuko la Manase anakhala m'dziko; anachuluka kuyambira Basani kufikira Baala-Heremoni, ndi Seniri, ndi phiri la Heremoni. Ndipo akulu a nyumba za makolo ao ndi awa: Efere, ndi Isi, ndi Eliyele, ndi Aziriele, ndi Yeremiya, ndi Hodaviya, ndi Yadiyele, anthu amphamvu ndithu, anthu omveka, akulu a nyumba za makolo ao. Koma analakwira Mulungu wa makolo ao, nachita chigololo, ndi kutsata milungu ya mitundu ya anthu a m'dziko, amene Mulungu adaononga pamaso pao. Ndipo Mulungu wa Israele anautsa mzimu wa Pulo mfumu ya Asiriya, ndi mzimu wa Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, ndiye anawatenga ndende; ndiwo Arubeni, ndi Agadi, ndi fuko la Manase logawika pakati, nafika nao ku Hala, ndi Habori, ndi Hara ndi ku mtsinje wa Gozani, mpaka lero lino. Ana a Levi: Geresomo, Kohati, ndi Merari. Ndi ana a Kohati: Amuramu, Izihara, ndi Hebroni, ndi Uziyele. Ndi ana a Amuramu: Aroni, ndi Mose, ndi Miriyamu. Ndi ana a Aroni: Nadabu, ndi Abihu, Eleazara, ndi Itamara. Eleazara anabala Finehasi, Finehasi anabala Abisuwa, ndi Abisuwa anabala Buki, ndi Buki anabala Uzi, ndi Uzi anabala Zerahiya, ndi Zerahiya anabala Meraiyoti, Meraiyoti anabala Amariya, ndi Amariya anabala Ahitubi, ndi Ahitubi anabala Zadoki, ndi Zadoki anabala Ahimaazi, ndi Ahimaazi anabala Azariya, ndi Azariya anabala Yohanani, ndi Yohanani anabala Azariya (ndiye amene anachita ntchito ya nsembe m'nyumba anaimanga Solomoni m'Yerusalemu), ndi Azariya anabala Amariya, ndi Amariya anabala Ahitubi, ndi Ahitubi anabala Zadoki, ndi Zadoki anabala Salumu, ndi Salumu anabala Hilikiya, ndi Hilikiya anabala Azariya, ndi Azariya anabala Seraya, ndi Seraya anabala Yehozadaki, ndi Yehozadaki analowa undende muja Yehova anatenga ndende Yuda ndi Yerusalemu ndi dzanja la Nebukadinezara. Ana a Levi: Geresomo, Kohati ndi Merari. Ndipo maina a ana a Geresomo ndi awa: Libini, ndi Simei. Ndipo ana a Kohati ndiwo Amuramu, ndi Izihara, ndi Hebroni, ndi Uziyele. Ana a Merari: Mali ndi Musi. Ndi mabanja a Alevi monga mwa nyumba za makolo ao ndi awa. Wa Geresomo: Libini mwana wake, Yahati mwana wake, Zima mwana wake, Yowa mwana wake, Ido mwana wake, Zera mwana wake, Yeterai mwana wake. Ana a Kohati: Aminadabu mwana wake, Kora mwana wake, Asiri mwana wake, Elikana mwana wake, ndi Ebiyasafu mwana wake, ndi Asiri mwana wake, Tahati mwana wake, Uriyele mwana wake, Uziya mwana wake, ndi Shaulo mwana wake. Ndi ana a Elikana: Amasai, ndi Ahimoti. Elikana: ana a Elikana Zofai mwana wake, ndi Nahati mwana wake, Eliyabu mwana wake, Yerohamu mwana wake, Elikana mwana wake. Ndi ana a Samuele: woyamba Yowele, ndi wachiwiri Abiya. Ana a Merari: Mali, Libini mwana wake, Simei mwana wake, Uza mwana wake, Simea mwana wake, Hagiya mwana wake, Asaya mwana wake. Ndipo iwo aja Davide anawaimika a udindo wa nyimbo m'nyumba ya Yehova, litafikira kupumula likasalo, ndi awa. Ndipo anatumikira ndi kuimba pakhomo pa Kachisi wa chihema chokomanako mpaka Solomoni adamanga nyumba ya Yehova m'Yerusalemu, naimirira m'utumiki wao monga mwa malongosoledwe ao. Ndipo oimirirawo, ndi ana ao, ndi awa: a ana a Akohati, Hemani woimbayo, mwana wa Yowele, mwana wa Samuele, mwana wa Elikana, mwana wa Yerohamu, mwana wa Eliyele, mwana wa Towa, mwana wa Zufu, mwana wa Elikana, mwana wa Mahati, mwana wa Amasai, mwana wa Elikana, mwana wa Yowele, mwana wa Azariya, mwana wa Zefaniya, mwana wa Tahati, mwana wa Asiri, mwana wa Ebiyasafu, mwana wa Kora, mwana wa Izihara, mwana wa Kohati, mwana wa Levi, mwana wa Israele. Ndi mbale wake Asafu wokhala ku dzanja lake lamanja, ndiye Asafu mwana wa Berekiya, mwana wa Simea, mwana wa Mikaele, mwana wa Baaseiya, mwana wa Malikiya, mwana wa Etini, mwana wa Zera, mwana wa Adaya, mwana wa Etani, mwana wa Zima, mwana wa Simei, mwana wa Yahati, mwana wa Geresomo, mwana wa Levi. Ndi ku dzanja lamanzere abale ao ana a Merari: Etani mwana wa Kisi, mwana wa Abidi, mwana wa Maluki, mwana wa Hasabiya, mwana wa Amaziya, mwana wa Hilikiya, mwana wa Amizi, mwana wa Bani, mwana wa Semeri, mwana wa Mali, mwana wa Musi, mwana wa Merari, mwana wa Levi. Ndi abale ao Alevi anaikidwa achite za utumiki zilizonse za Kachisi wa nyumba ya Mulungu. Koma Aroni ndi ana ake ankafukiza pa guwa la nsembe yopsereza, ndi pa guwa la nsembe yofukiza, chifukwa cha ntchito yonse ya malo opatulika kwambiri, ndi kuchitira Israele chowatetezera, monga mwa zonse Mose mtumiki wa Mulungu adawauza. Ndipo ana a Aroni ndiwo Eleazara mwana wake, Finehasi mwana wake, Abisuwa mwana wake, Buki mwana wake, Uzi mwana wake, Zerahiya mwana wake, Meraiyoti mwana wake, Amariya mwana wake, Ahitubi mwana wake, Zadoki mwana wake, Ahimaazi mwana wake. Pokhala pao tsono monga mwa madera ao m'malire mwao ndi awa: kwa ana a Aroni a mabanja a Akohati, pakuti maere oyamba adagwera iwowa, kwa iwo anapereka Hebroni m'dziko la Yuda, ndi podyetsa pake pozungulira pake; koma minda ya mudzi ndi milaga yake anapatsa Kalebe mwana wa Yefune. Ndi kwa ana a Aroni anapereka midzi yopulumukirako: Hebroni, ndi Libina ndi mabusa ake, ndi Yatiri, ndi Esitemowa ndi mabusa ake. Ndi Hileni ndi mabusa ake, ndi Debiri ndi mabusa ake, ndi Asani ndi mabusa ake, ndi Betesemesi ndi mabusa ake; ndi ku fuko la Benjamini Geba ndi mabusa ake, ndi Alemeti ndi mabusa ake, ndi Anatoti ndi mabusa ake. Midzi yao yonse mwa mabanja ao ndiyo midzi khumi ndi itatu. Ndipo otsala a ana a Kohati analandira mwa maere, motapa pa mabanja a fuko, pa fuko la Manase logawika pakati, midzi khumi. Ndi kwa ana a Geresomo monga mwa mabanja ao, motapa pa fuko la Isakara, ndi pa fuko la Asere, ndi pa fuko la Nafutali, ndi pa fuko la Manase m'Basani, midzi khumi ndi itatu. Ana a Merari analandira mwa maere monga mwa mabanja ao, motapa pa fuko la Rubeni, ndi pa fuko la Gadi, ndi pa fuko la Zebuloni, midzi khumi ndi iwiri. Ndipo ana a Israele anapatsa Alevi midzi ndi mabusa ao. Ndipo anapatsa mwamaere, motapa pa fuko la ana a Yuda, ndi pa fuko la Simeoni, ndi pa fuko la ana a Benjamini, midzi iyi yotchulidwa maina ao. Ndi mabanja ena a ana a Kohati anali nayo midzi ya malire ao, yotapa pa fuko la Efuremu. Ndipo anawapatsa midzi yopulumukiramo: Sekemu ndi mabusa ake ku mapiri a Efuremu, Gezere ndi mabusa ake, ndi Yokomeamu ndi mabusa ake, ndi Betehoroni ndi mabusa ake, ndi Ayaloni ndi mabusa ake, ndi Gatirimoni ndi mabusa ake, ndi motapa pa fuko la Manase logawika pakati, Anere ndi mabusa ake, ndi Bileamu ndi mabusa ake, kwa otsala a mabanja a ana a Kohati. Ana a Geresomo analandira motapa pa mabanja a fuko la Manase logawika pakati, Golani m'Basani ndi mabusa ake, ndi Asitaroti ndi mabusa ake; ndi motapa pa fuko la Isakara, Kedesi ndi mabusa ake, Daberati ndi mabusa ake, ndi Ramoti ndi mabusa ake, ndi Anemu ndi mabusa ake; ndi motapa pa fuko la Asere, Masala ndi mabusa ake, ndi Abidoni ndi mabusa ake, ndi Hukoki ndi mabusa ake, ndi Rehobu ndi mabusa ake; ndi motapa pa fuko la Nafutali, Kedesi m'Galileya ndi mabusa ake, ndi Hamoni ndi mabusa ake, ndi Kiriyataimu ndi mabusa ake. Amerari (otsala a Alevi) analandira, motapa pa fuko la Zebuloni, Rimoni ndi mabusa ake, Tabori ndi mabusa ake; ndi tsidya lija la Yordani kum'mawa kwa Yeriko analandira, motapa pa fuko la Rubeni, Bezeri m'chipululu ndi mabusa ake, ndi Yahazi ndi mabusa ake, ndi Kedemoti ndi mabusa ake, ndi Mefaati ndi mabusa ake; ndi motapa m'fuko la Gadi, Ramoti m'Giliyadi ndi mabusa ake, ndi Mahanaimu ndi mabusa ake, ndi Hesiboni ndi mabusa ake, ndi Yazere ndi mabusa ake. Ana a Isakara ndiwo Tola, ndi Puwa, Yasubu ndi Simironi; anai. Ndi ana a Tola: Uzi, ndi Refaya, ndi Yeriyele, ndi Yamai, ndi Ibisamu, ndi Semuele, akulu a nyumba za makolo; ao ndiwo a Tola, ngwazi zamphamvu, m'mibadwo yao; kuwerenga kwao, masiku a Davide ndiko zikwi makumi awiri mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi limodzi. Ndi mwana wa Uzi: Izrahiya; ndi ana a Izrahiya: Mikaele, ndi Obadiya, ndi Yowele, ndi Isiya; onse asanuwa ndiwo akulu. Ndi pamodzi nao mwa mibadwo yao, mwa nyumba za makolo ao, panali magulu a nkhondo zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi chimodzi, popeza anachuluka akazi ao ndi ana ao. Ndi abale ao mwa mabanja onse a Isakara, ngwazi zamphamvu, oyesedwa mwa chibadwidwe chao, onsewa ndiwo zikwi zisanu ndi zitatu mphambu zisanu ndi ziwiri. Ana a Benjamini ndiwo Bela, ndi Bekere, ndi Yediyaele, atatu. Ndi ana a Bela: Eziboni, ndi Uzi, ndi Uziyele, ndi Yerimoti, ndi Iri, asanu; akulu a nyumba za makolo ao, ngwazi zamphamvu, owerengedwa m'mabuku a chibadwidwe zikwi makumi awiri mphambu ziwiri kudza makumi atatu ndi anai. Ndi ana a Bekere: Zimira, ndi Yowasi, ndi Eliyezere, ndi Eliyoenai, ndi Omuri, ndi Yeremoti, ndi Abiya, ndi Anatoti, ndi Alemeti. Onsewa ndiwo ana a Bekere. Ndipo anayesedwa mwa chibadwidwe chao, mwa mibadwo yao, akulu a nyumba za makolo ao, ngwazi zamphamvu zikwi makumi awiri mphambu mazana awiri. Ndi mwana wa Yediyaele: Bilihani; ndi ana a Bilihani: Yeusi, ndi Benjamini, ndi Ehudi, ndi Kenana, ndi Zetani, ndi Tarisisi, ndi Ahisahara. Onsewa ndiwo ana a Yediyaele; ndiwo akulu a nyumba za makolo ao, ngwazi zamphamvu zikwi khumi mphambu zisanu ndi ziwiri kudza mazana awiri akutuluka kugulu kunkhondo. Supimu yemwe ndi Hupimu ana a Iri, ndi Husimu mwana wa Aheri. Ana a Nafutali: Yaziyele, ndi Guni, ndi Yezere, ndi Salumu, ana a Biliha. Ana a Manase ndiwo Asiriele amene mkazi wake anambala. Koma mkazi wake wamng'ono Mwaramu anabala Makiri atate wa Giliyadi; ndi Makiri anadzitengera mkazi, mlongo wake wa Hupimu ndi Supimu, dzina lake ndiye Maaka. Ndipo dzina la mwana wachiwiri wa Manase ndiye Zelofehadi. Ndi Zelofehadi anali ndi ana akazi. Ndi Maaka mkazi wa Makiri anabala mwana, namutcha dzina lake Peresi, ndi dzina la mbale wake ndiye Seresi, ndi ana ake ndiwo Ulamu, ndi Rakemu. Ndi mwana wa Ulamu: Bedani; ndiwo ana a Giliyadi mwana wa Makiri mwana wa Manase. Ndi mlongo wake Hamoleketi anabala Isihodi, ndi Abiyezere, ndi Mala. Ndi ana a Semida ndiwo Ahiyani, ndi Sekemu, ndi Liki, ndi Aniyamu. Ndi ana a Efuremu: Sutela, ndi Beredi mwana wake, ndi Tahati mwana wake, ndi Eleada mwana wake, ndi Tahati mwana wake, ndi Zabadi mwana wake, ndi Sutela mwana wake, ndi Ezere, ndi Eleadi, amene anthu a Gati obadwa m'dziko anamupha, popeza anatsikira kukalanda zoweta zao. Ndipo Efuremu atate wao, anachita maliro masiku ambiri, ndi abale ake anadza kudzamtonthoza mtima. Ndipo analowa kwa mkazi wake, naima iye, nabala mwana, namutcha dzina lake Beriya, popeza m'nyumba mwake mudaipa. Ndipo mwana wake wamkazi ndiye Seera, amene anamanga Betehoroni wa kunsi, ndi Betehoroni wa kumtunda, ndi Uzeniseera. Ndipo Refa anali mwana wake, ndi Resefi, ndi Tela mwana wake, ndi Tahani mwana wake, Ladani mwana wake, Amihudi mwana wake, Elisama mwana wake, Nuni mwana wake, Yoswa mwana wake. Ndipo dziko lao, ndi pokhala pao ndizo Betele ndi milaga yake, ndi kum'mawa Naarani, ndi kumadzulo Gezere ndi milaga yake, ndi Sekemu ndi milaga yake, mpaka Aya ndi milaga yake; ndi kumalire a ana a Manase; Beteseani ndi milaga yake, Taanaki ndi milaga yake, Megido ndi milaga yake, Dori ndi milaga yake. M'menemo anakhala ana a Yosefe mwana wa Israele. Ana a Asere: Imina, ndi Isiva, ndi Isivi, ndi Beriya, ndi Sera mlongo wao. Ndi ana a Beriya: Hebere, ndi Malikiele, ndiye atate wa Birizaiti. Ndi Hebere anabala Yafileti, ndi Somere, ndi Hotamu, ndi Suwa mlongo wao. Ndi ana a Yafileti: Pasaki, ndi Bimala, ndi Asivati. Awa ndi ana a Yafileti. Ndi ana a Semeri: Ahi, ndi Roga, Yehuba, ndi Aramu. Ndi ana a Helemu mbale wake: Zofa, ndi Imina, ndi Selesi, ndi Amala. Ana a Zofa: Suwa, ndi Harenefere, ndi Suwala, ndi Beri, ndi Imira, Bezere, ndi Hodi, ndi Sama, ndi Silisa, ndi Itirani, ndi Beera. Ndi ana a Yetere: Yefune, ndi Pisipa, ndi Ara. Ndi ana a Ula: Ara, ndi Haniyele, ndi Riziya. Awa onse ndiwo ana a Asere, akulu a nyumba za makolo ao, ngwazi zosankhika ndi zamphamvu, akulu mwa akalonga. Oyesedwa mwa chibadwidwe chao otumikira kunkhondo ndiwo amuna zikwi makumi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi. Ndipo Benjamini anabala Bela mwana wake woyamba, Asibele wachiwiri, ndi Ahara wachitatu, Noha wachinai, ndi Rafa wachisanu. Ndi Bela anali ndi ana: Adara, ndi Gera, ndi Abihudi, ndi Abisuwa, ndi Naamani, ndi Ahowa, ndi Gera, ndi Sefufani, ndi Huramu. Ndi ana a Ehudi ndi awa: ndiwo akulu a nyumba za makolo ao a iwo okhala ku Geba, ndipo anawatenga ndende kunka ku Manahati, natenga ndende Naamani, ndi Ahiya, ndi Gera, ndipo, anabala Uza, ndi Ahihudi. Ndipo Saharaimu anabala ana ku dziko la Mowabu, atachotsa akazi ake Husimu ndi Baara. Ndipo Hodesi mkazi wake anambalira Yobabu, ndi Zibiya, ndi Mesa, ndi Malikamu, ndi Yeuzi, ndi Sakiya, ndi Mirima. Awa ndi ana ake akulu a nyumba za makolo ao. Ndi Husimu anambalira Abitubu, ndi Elipaala. Ndi ana a Elipaala: Eberi, ndi Misamu, ndi Semedi, amene anamanga Ono, ndi Lodi ndi milaga yake, ndi Beriya, ndi Sema; ndiwo akulu a nyumba za makolo a iwo okhala m'Ayaloni, amene anathawitsa okhala m'Gati; ndi Ahiyo, Sasaki, ndi Yeremoti, ndi Zebadiya, ndi Aradi, ndi Edere, ndi Mikaele, ndi Isipa, ndi Yoha, ana a Beriya; ndi Zebadiya, ndi Mesulamu, ndi Hiziki, ndi Hebere, ndi Isimerai, ndi Iziliya, ndi Yobabu, ana a Elipaala; ndi Yakimu, ndi Zikiri, ndi Zabidi, ndi Eliyenai, ndi Ziletai, ndi Eliyele, ndi Adaya, ndi Beraya, ndi Simiratu, ana a Simei; ndi Isipani, ndi Eberi, ndi Eliyele, ndi Abidoni, ndi Zikiri, ndi Hanani, ndi Hananiya, ndi Elamu, ndi Antotiya, ndi Ifidea, ndi Penuwele, ana a Sasaki; ndi Samuserai, ndi Sehariya, ndi Ataliya, ndi Yaaresiya ndi Eliya, ndi Zikiri, ana a Yerohamu. Awa ndi akulu a nyumba za makolo mwa mibadwo yao, ndiwo akulu anakhala m'Yerusalemu awa. Ndipo m'Gibiyoni anakhala atate a Gibiyoni, dzina la mkazi wake ndiye Maaka; ndi mwana wake woyamba ndiye Abidoni, opondana naye ndi Zuri, ndi Kisi, ndi Baala, ndi Nadabu, ndi Gedori, ndi Ahiyo, ndi Zekeri. Ndipo Mikiloti anabala Simea. Ndi iwonso anakhala pamodzi ndi abale ao m'Yerusalemu, popenyana ndi abale ao. Ndipo Nere anabala Kisi, ndi Kisi anabala Saulo, ndi Saulo anabala Yonatani, ndi Malikisuwa, ndi Abinadabu, ndi Esibaala. Ndi mwana wa Yonatani, ndiye Meribaala; ndi Meribaala anabala Mika. Ndi ana a Mika: Pitoni, ndi Meleki, ndi Tareya, ndi Ahazi. Ndi Ahazi anabala Yehoyada, ndi Yehoyada anabala Alemeti, ndi Azimaveti, ndi Zimiri; ndi Zimiri anabala Moza; ndi Moza anabala Bineya, mwana wake ndiye Rafa, mwana wake Eleasa, mwana wake Azele; ndipo Azele anali nao ana asanu ndi mmodzi, maina ao ndiwo Azirikamu, Bokeru, ndi Ismaele, ndi Seyariya, ndi Obadiya, ndi Hanani. Onsewa ndiwo ana a Azele. Ndipo ana a Eseki mbale wake: Ulamu mwana wake woyamba, Yeusi wachiwiri, ndi Elifeleti wachitatu. Ndipo ana a Ulamu ndiwo ngwazi zamphamvu, ndiwo oponya mivi, nakhala nao ana ambiri ndi zidzukulu zana limodzi. Onsewa ndiwo a ana a Benjamini. Ndipo Aisraele onse anawerengedwa mwa chibadwidwe chao; ndipo taonani, alembedwa m'buku la mafumu a Israele; ndipo Yuda anatengedwa ndende kunka ku Babiloni chifukwa cha kulakwa kwao. Okhala m'dziko oyamba tsono, akukhala mwaomwao m'midzi mwao, ndiwo Israele, ansembe, Alevi, ndi Anetini. Ndipo m'Yerusalemu munakhala a ana a Yuda, ndi a ana a Benjamini, ndi a ana a Efuremu ndi Manase: Utai mwana wa Amihudi, mwana wa Omuri, mwana wa Imuri, mwana wa Bani, wa ana a Perezi mwana wa Yuda. Ndipo a Asiloni: Asaya woyamba, ndi ana ake. Ndi a ana a Zera: Yeuwele ndi abale ao mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi anai. Ndi a ana a Benjamini: Salu mwana wa Mesulamu, mwana wa Hodaviya, mwana wa Hasenuwa; ndi Ibineya mwana wa Yerohamu, ndi Ela mwana wa Uzi, mwana wa Mikiri, ndi Mesulamu mwana wa Sefatiya, mwana wa Reuwele, mwana wa Ibineya, ndi abale ao monga mwa mibadwo yao mazana asanu ndi anai mphambu makumi asanu kudza asanu ndi mmodzi. Onsewa ndiwo akulu a nyumba za makolo ao m'nyumba za makolo ao. Ndi a ansembe: Yedaya, ndi Yehoyaribu, ndi Yakini, ndi Azariya mwana wa Hilikiya, mwana wa Mesulamu, mwana wa Zadoki, mwana wa Meraiyoti, mwana wa Ahitubi, mtsogoleri wa m'nyumba ya Mulungu; ndi Adaya mwana wa Yerohamu, mwana wa Pasuri, mwana wa Malikiya, ndi Maasai mwana wa Adiyele, mwana wa Yazera, mwana wa Mesulamu, mwana wa Mesilemiti, mwana wa Imeri, ndi abale ao, akulu a nyumba za makolo ao chikwi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi limodzi, anthu odziwitsitsa ntchito ya utumiki wa nyumba ya Mulungu. Ndi a Alevi: Semaya mwana wa Hasubu, mwana wa Azirikamu, mwana wa Hasabiya, a ana a Merari; ndi Bakibakara, Heresi, ndi Galali, ndi Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zikiri, mwana wa Asafu; ndi Obadiya mwana wa Semaya, mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni, ndi Berekiya mwana wa Asa, mwana wa Elikana, wokhala m'midzi ya Anetofa. Ndi odikira pakhomo: Salumu, ndi Akubu, ndi Talimoni, ndi Ahimani ndi abale ao; Salumu ndi mkulu wao, amene adadikira pa chipata cha mfumu kum'mawa mpaka pomwepo, ndiwo odikira pakhomo a tsasa la ana a Levi. Ndipo Salumu mwana wa Kore, mwana wa Ebiyasafu, mwana wa Kora, ndi abale ake a nyumba ya atate wake; Akora anayang'anira ntchito ya utumiki, osunga zipata za Kachisi monga makolo ao; anakhala m'chigono cha Yehova osunga polowera; ndi Finehasi mwana wa Eleazara anali mtsogoleri wao kale, ndipo Yehova anali naye. Zekariya mwana wa Meselemiya anali wodikira pakhomo pa chihema chokomanako. Iwo onse osankhidwa akhale odikira kuzipata ndiwo mazana awiri mphambu khumi ndi awiri. Iwo anawerengedwa monga mwa chibadwidwe chao, m'midzi mwao, amene Davide ndi Samuele mlauli anawaika m'udindo wao. Momwemo iwo ndi ana ao anayang'anira zipata za kunyumba ya Yehova, ndiyo nyumba ya Kachisi, m'udikiro wao. Pa mbali zinai panali odikira kum'mawa, kumadzulo, kumpoto, ndi kumwera. Ndi abale ao m'midzi mwao akafikafika, atapita masiku asanu ndi awiri masabata onse, kuti akhale nao; pakuti odikira anai akulu, ndiwo Alevi, anali m'udindo wao, nayang'anira zipinda ndi mosungiramo chuma m'nyumba ya Mulungu. Ndipo amagona usiku m'zipinda zozinga nyumba ya Mulungu, popeza udikiro wake ndi wao; kuitsegula m'mawa ndi m'mawa ndi kwaonso. Ndi ena a iwo anayang'anira zipangizo za utumikiwo, pakuti analowa nazo ataziwerenga, natuluka nazo ataziwerenga. Ndi ena a iwo anaikidwa ayang'anire zipangizo zilizonse, ndi zipangizo zonse za malo opatulika, ndi ufa wosalala, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi lubani, ndi zonunkhira. Ndi ana ena a ansembe anasanganiza chisanganizo cha zonunkhira. Ndi Matitiya wina wa Alevi, ndiye mwana woyamba wa Salumu Mkora, anaikidwa ayang'anire zokazingidwa m'ziwaya. Ndi ena a abale ao, a ana a Akohati, anayang'anira mkate woonekera, kuukonza masabata onse. Ndipo awa ndi oimba akulu a nyumba za makolo a Alevi, okhala m'zipinda, omasuka ku ntchito zina; pakuti anali nayo ntchito yao usana ndi usiku. Awa ndi akulu a nyumba za makolo a Alevi mwa mibadwo yao, ndiwo akulu; anakhala ku Yerusalemu awa. Ndipo m'Gibiyoni munakhala atate wa Gibiyoni Yeiyele, dzina la mkazi wake ndiye Maaka; ndi mwana wake woyamba ndiye Abidoni, opondana naye ndi Zuri, ndi Kisi, ndi Baala, ndi Nere, ndi Nadabu, ndi Gedori, ndi Ahiyo, ndi Zekariya, ndi Mikiloti. Ndi Mikiloti anabala Simeamu. Ndipo iwonso anakhala pamodzi ndi abale ao m'Yerusalemu, pandunji pa abale ao. Ndipo Nere anabala Kisi, ndi Kisi anabala Saulo, ndi Saulo anabala Yonatani, ndi Malikisuwa, ndi Abinadabu, ndi Esibaala. Ndipo mwana wa Yonatani ndiye Meribaala; ndi Meribaala anabala Mika. Ndi ana a Mika: Pitoni, ndi Meleki, ndi Tareya, ndi Ahazi. Ndi Ahazi anabala Yara, ndi Yara anabala Alemeti, ndi Azimaveti, ndi Zimiri; ndi Zimiri anabala Moza, ndi Moza anabala Bineya, ndi Refaya mwana wake, Eleasa mwana wake, Azele mwana wake; ndi Azele anali nao ana asanu ndi mmodzi, maina ao ndi awa; Azirikamu, Bokeru, ndi Ismaele, ndi Seyariya, ndi Obadiya, ndi Hanani; awa ndi ana a Azele. Afilisti tsono analimbana nkhondo ndi Israele; ndipo amuna a Israele anathawa pamaso pa Afilisti, nagwa ophedwa pa phiri la Gilibowa. Ndipo Afilisti anaumirira kutsata Saulo ndi ana ake, ndi Afilistiwo anawapha Yonatani, ndi Abinadabu, ndi Malikisuwa, ana a Saulo. Ndi nkhondoyi inamkulira Saulo, ndi amauta anampeza; ndipo anatenga nkhawa chifukwa cha amauta. Pamenepo Saulo anati kwa wonyamula zida zake, Solola lupanga lako, nundipyoze nalo, angafike osadulidwa awa ndi kundiseka. Koma wonyamula zida zake anakana, popeza anaopa kwambiri. Pomwepo Saulo anatenga lupanga lake, naligwera. Ndipo pamene wonyamula zida zake anaona kuti Saulo wafa, anagwera nayenso lupanga lake, nafa. Momwemo anafa Saulo, ndi ana ake atatu; ndi nyumba yake yonse idafa pamodzi. Ndipo pamene amuna onse a Israele okhala m'chigwamo anaona kuti anathawa, ndi kuti Saulo ndi ana ake adafa, anasiya midzi yao, nathawa; nadza Afilisti, nakhala m'menemo. Ndipo m'mawa mwake anafika Afilisti kuvula za ophedwa, napeza Saulo ndi ana ake adagwa pa phiri la Gilibowa. Ndipo anamvula natenga mutu wake, ndi zida zake, natumiza ku dziko la Afilisti pozungulirapo, kulalika m'mafano ao ndi mwa anthu. Ndipo anaika zida zake m'nyumba ya milungu yao, napachika mutu wake m'nyumba ya Dagoni. Ndipo onse a Yabesi-Giliyadi, atamva zonse Afilisti adachitira Saulo, anauka ngwazi zonse, nachotsa mtembo wa Saulo, ndi mitembo ya ana ake, nabwera nayo ku Yabesi, naika mafupa ao patsinde pa mtengo wathundu ku Yabesi, nasala masiku asanu ndi awiri. Momwemo Saulo anafa, chifukwa cha kulakwa kwake analakwira Yehova, kulakwira mau a Yehova amene sanawasunge; ndiponso chifukwa cha kufunsira wobwebweta, kufunsirako, osafunsira kwa Yehova; chifukwa chake anamupha, napambutsira ufumu kwa Davide mwana wa Yese. Pamenepo Aisraele onse anasonkhana kwa Davide ku Hebroni, ndi kuti, Taonani, ife ndife fupa lanu, ndi mnofu wanu. Ngakhale kale lomwe, pokhala mfumu Sauloyo, wotuluka ndi kulowa nao Aisraele ndinu; ndipo Yehova Mulungu wanu anati kwa inu, Uzidyetsa anthu anga Aisraele, nukhale mtsogoleri wa anthu anga Israele. Akulu onse omwe a Israele anadza kwa mfumu ku Hebroni; ndipo Davide anapangana nao pangano ku Hebroni pamaso pa Yehova; ndipo anamdzoza Davide akhale mfumu ya Israele monga mwa mau a Yehova, ndi dzanja la Samuele. Namuka Davide ndi Aisraele onse naye ku Yerusalemu, ndiwo Yebusi; ndipo Ayebusi nzika za m'dziko zinali komweko. Ndipo nzika za m'Yebusi zinati kwa Davide, Sungalowe muno. Koma Davide analanda linga la Ziyoni, ndiwo mudzi wa Davide. Nati Davide, Aliyense woyamba kukantha Ayebusi, yemweyo adzakhala mkulu ndi mtsogoleri. Nayamba kukwerako Yowabu mwana wa Zeruya, nakhala mkulu iyeyu. Ndipo Davide anakhala m'lingamo; chifukwa chake analitcha mudzi wa Davide. Ndipo anamanga mudzi pozungulira pake, kuyambira ku Milo ndi pozungulira pake; ndi Yowabu anakonzanso potsala pa mudzi. Ndipo Davide anakulakulabe, pakuti Yehova wa makamu anali naye. Akulu a amphamvu aja Davide anali nao akulimbika pamodzi naye m'ufumu wake, pamodzi ndi Aisraele onse, kumlonga ufumu, monga mwa mau a Yehova akunena za Israele, ndi awa. Kuwerenga kwa amphamvu aja Davide anali nao ndi uku: Yasobeamu mwana wa Muhakimoni, mkulu wa makumi atatu aja, anasamulira mazana atatu mkondo wake, nawapha nthawi imodzi. Ndi pambuyo pake Eleazara mwana wa Dodo Mwahohi, ndiye mmodzi wa atatu aja amphamvu. Anali pamodzi ndi Davide ku Pasidamimu muja; Afilisti anasonkhanako kunkhondo kumene kunali munda wodzala ndi barele; ndipo anthu anathawa pamaso pa Afilisti. Koma anadziimika pakati pa munda, naulanditsa, nakantha Afilisti; m'mwemo anawapulumutsa Yehova ndi chipulumutso chachikulu. Ndipo atatu a akulu makumi atatu anatsikira kuthanthwe kwa Davide, ku phanga la Adulamu; ndi nkhondo ya Afilisti idamanga misasa m'chigwa cha Refaimu. Pamenepo Davide anali m'linga, ndi boma la asilikali a Afilisti linali ku Betelehemu. Ndipo Davide analakalaka, nati, Ha? Mwenzi wina atandimwetsa madzi a m'chitsime cha ku Betelehemu chili kuchipata. Napyola atatuwo misasa ya Afilisti natunga madzi ku chitsime cha ku Betelehemu chili kuchipata, nabwera nao kwa Davide; koma Davide anakana kumwako, koma anawathirira kwa Yehova; nati, Pali Mulungu wanga, kukhale kutali kwa ine kuchita ichi. Ngati ndidzamwa mwazi wa anthu awa? Akadataya moyo wao, inde akadataya moyo wao, pakukatenga madziwa. M'mwemo sanafune kuwamwa. Izi anazichita atatu amphamvuwa. Ndipo Abisai mbale wa Yowabu, ndiye wamkulu wa atatuwa; pakuti anasamulira mazana atatu mkondo wake, nawapha, namveka dzina pakati pa atatuwa. Mwa atatuwa iye anali waulemu woposa awiriwa, nasanduka mkulu wao; koma sanafike pa atatu oyamba aja. Benaya mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi ya ku Kabizeeli, wochita zachikulu, anapha ana awiri a Ariyele wa ku Mowabu; anatsikanso, napha mkango m'kati mwa dzenje nyengo ya chipale chofewa. Anaphanso Mwejipito munthu wamkulu, msinkhu wake mikono isanu, ndi m'dzanja la Mwejipito munali mkondo ngati mtanda woombera nsalu; ndipo anamtsikira ndi ndodo, nakwatula mkondo m'dzanja la Mwejipito, namupha ndi mkondo wake womwe. Izi anazichita Benaya mwana wa Yehoyada, namveka dzina mwa atatu amphamvuwo. Taonani, anali wa ulemu woposa makumi atatuwo, koma sanafike pa atatu oyamba aja; ndipo Davide anamuika mkulu wa olindirira ake. Ndipo amphamvuwo a magulu a nkhondo ndiwo Asahele mbale wa Yowabu, Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu, Samoti Muharodi, Helezi Mpeloni, Ira mwana wa Ikesi wa ku Tekowa, Abiyezere wa ku Anatoti, Sibekai Muhusa, Ilai Mwahohi, Maharai Mnetofa, Heledi mwana wa Baana Mnetofa, Itai mwana wa Ribai wa Gibea wa ana a Benjamini, Benaya Mpiratoni, Hurai wa ku mitsinje ya Gaasi, Abiyele Mwarabati, Azimaveti Mbaharumi, Eliyaba Msaaliboni; ana a Hasemu Mgizoni; Yonatani mwana wa Sage Muharari, Ahiyamu mwana wa Sakara Muharari, Elifala mwana wa Uri, Hefere Mmekerati, Ahiya Mpeloni, Heziro wa ku Karimele, Naarai mwana wa Ezibai, Yowele mbale wa Natani, Mibara mwana wa Hagiri, Zeleki Mwamoni, Naharai Mbeeroti wonyamula zida za Yowabu mwana wa Zeruya, Ira Mwitiri, Garebu Mwitiri, Uriya Muhiti, Zabadi mwana wa Alai, Adina mwana wa Siza Mrubeni mkulu wa Arubeni, ndi makumi atatu pamodzi naye, Hanani mwana wa Maaka, ndi Yosafati Mmitini, Uziya Mwasiterati, Sama ndi Yeiyele ana a Hotamu wa ku Aroere, Yediyaele mwana wa Simiri, ndi Yoha mbale wake Mtizi, Eliyele Mmahavi, ndi Yeribai ndi Yosaviya ana a Elinaamu, ndi Itima Mmowabu, Eliyele, ndi Obedi, ndi Yaasiyele Mmezobai. Anadzawo kwa Davide ku Zikilagi, akali chitsekedwere chifukwa cha Saulo mwana wa Kisi, ndi awa; ndiwo mwa amphamvuwo omthandiza kunkhondo. Anakoka mauta; naponya miyala, naponya mivi ndi uta ndi dzanja lamanja ndi lamanzere lomwe; ndiwo a abale ake a Saulo, Abenjamini. Mkulu wao ndiye Ahiyezere, ndi Yowasi, ana a Semaa wa ku Gibea; ndi Yeziyele, ndi Peleti, ana a Azimaveti; ndi Beraka, ndi Yehu wa ku Anatoti, ndi Isimaya wa ku Gibiyoni, wamphamvu mwa makumi atatuwo ndi woyang'anira makumi atatuwo, ndi Yeremiya, ndi Yahaziele, ndi Yohanani, ndi Yozabadi wa ku Gedera, Eluzai, ndi Yerimoti, ndi Bealiya, ndi Semariya, ndi Sefatiya wa ku Harufi, Elikana, ndi Isiya, ndi Azarele, ndi Yowezere, ndi Yasobeamu ndiwo Akora; ndi Yowela, ndi Zebadiya, ana a Yerohamu wa ku Gedori. Ndi Agadi ena anapatukira kwa Davide ku linga la m'chipululu, ngwazi zamphamvu zozerewera nkhondo, zogwira chikopa ndi mkondo; nkhope zao zikunga nkhope za mikango, ndi liwiro lao longa la ngoma mumapiri: Ezere mkulu wao, wachiwiri Obadiya, wachitatu Eliyabu, wachinai Misimana, wachisanu Yeremiya, wachisanu ndi chimodzi Atai, wachisanu ndi chiwiri Eliyele, wachisanu ndi chitatu Yohanani, wachisanu ndi chinai Elizabadi, wakhumi Yeremiya, wakhumi ndi chimodzi Makibanai. Awa a ana a Gadi, anali atsogoleri a nkhondo; wamng'ono wa iwo anayang'anira zana limodzi, ndi wamkulu wa iwo anayang'anira chikwi chimodzi. Awa ndi omwe aja anaoloka Yordani mwezi woyamba, atadzala kusefukira magombe ake onse; nathawitsa onse okhala m'zigwa kum'mawa ndi kumadzulo. Ndipo anadza ena a ana a Benjamini ndi Yuda kulinga kwa Davide. Ndipo Davide anatuluka kukomana nao, nayankha, nanena nao, Ngati mwandidzera mwamtendere kundithandiza, mtima wanga udzalumikizana nanu; koma ngati mwafika kundipereka kwa adani anga, popeza m'manja mwanga mulibe chiwawa, Mulungu wa makolo athu achione ndi kuchilanga. Pamenepo mzimu unavala Amasai, ndiye wamkulu wa makumi atatuwo, nati iye, Ndife anu, Davide, tivomerezana nanu mwana wa Yese inu: mtendere, mtendere ukhale ndi inu, ndi mtendere ukhale ndi athandizi anu; pakuti Mulungu wanu akuthandizani. Ndipo Davide anawalandira, nawaika akulu a magulu. Ena a Manase omwe anapatukira kwa Davide, muja iye anadza ndi Afilisti koponyana nkhondo ndi Saulo, koma sanawathandiza; popeza akalonga a Afilisti, atachita upo, anamuuza achoke, ndi kuti, Adzapatukira kwa mbuye wake Saulo ndi kutisandulikira. Pomuka iye ku Zikilagi anapatukira kwa iye a Manase: Adina, ndi Yozabadi, ndi Yediyaele, ndi Mikaele, ndi Yozabadi, ndi Elihu, ndi Ziletai, akulu a zikwi a ku Manase. Ndipo anathandiza Davide aponyane nalo gulu la achifwamba, pakuti onse ndiwo ngwazi zamphamvu, nakhala atsogoleri m'khamu la nkhondo. Pakuti nthawi yomweyo anadza kwa Davide kumthandiza, mpaka kunali nkhondo yaikulu, ngati nkhondo ya Mulungu. Ndipo kuwerenga kwa akulu okonzekeratu kunkhondo, anadzawo kwa Davide ku Hebroni, kupambukitsa ufumu wa Saulo ukhale wake, monga mwa mau a Yehova, ndi uku. Ana a Yuda akunyamula zikopa ndi mikondo ndiwo zikwi zisanu ndi chimodzi mphambu mazana asanu ndi atatu, okonzekeratu kunkhondo. A ana a Simeoni ngwazi zamphamvu za nkhondo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu zana limodzi. A ana a Levi zikwi zinai mphambu mazana asanu ndi limodzi. Ndipo Yehoyada, ndiye mtsogoleri wa nyumba ya Aroni, ndi pamodzi naye zikwi zitatu mphambu mazana asanu ndi awiri; ndi Zadoki, ndiye mnyamata, ngwazi yamphamvu, ndi a nyumba ya kholo lake akulu makumi awiri mphambu awiri. Ndi a ana a Benjamini, abale a Saulo, zikwi zitatu; pakuti mpaka pomwepo ochuluka a iwowa anaumirira nyumba ya Saulo. Ndi a ana a Efuremu zikwi makumi awiri mphambu mazana asanu ndi atatu, ngwazi zamphamvu, anthu omveka m'nyumba za makolo ao. Ndipo a fuko la Manase logawika pakati zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu, otchulidwa maina ao kuti adzalonge Davide mfumu. Ndi a ana a Isakara, anthu akuzindikira nyengo, akudziwa zoyenera Israele kuzichita, akulu ao ndiwo mazana awiri; ndi abale ao onse anapenyerera pakamwa pao. A Zebuloni akutuluka kukhamu, opangira nkhondo, monga mwa zida zilizonse za nkhondo, zikwi makumi asanu, akusunga malongosoledwe a nkhondo ndi mtima wosatekeseka. Ndi a Nafutali atsogoleri chikwi chimodzi, ndi pamodzi nao ogwira zikopa ndi mikondo zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi ziwiri. Ndi a Adani akupangira nkhondo zikwi makumi awiri mphambu zisanu ndi zitatu kudza mazana asanu ndi limodzi. Ndi a Asere akutuluka kukhamu, akupangira nkhondo, zikwi makumi anai. Ndi tsidya lija la Yordani a Arubeni, ndi Agadi, ndi fuko la Manase logawika pakati, ndi zina zilizonse za khamu kuchita nazo nkhondo, zikwi zana limodzi ndi makumi awiri. Onsewa, ndiwo anthu a nkhondo akusunga malongosoledwe a nkhondo, anadza ku Hebroni ndi mtima wangwiro kudzamlonga Davide mfumu ya Aisraele onse; ndi onse otsala a Israele omwe anali a mtima umodzi kumlonga Davide ufumu. Ndipo anali komweko kwa Davide masiku atatu kudya ndi kumwa, popeza abale ao anazikonzeratu. Ndiponso akuyandikizana nao mpaka Isakara ndi Zebuloni ndi Nafutali anabwera nao mkate osenzetsa abulu, ndi ngamira, ndi nyuru, ndi ng'ombe, zakudya zaufa, ndi nchinchi zankhuyu, ndi nchinchi zamphesa, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi ng'ombe, ndi nkhosa zochuluka; pakuti munali chimwemwe m'Israele. Ndipo Davide anafunsana ndi akulu a zikwi ndi a mazana, inde atsogoleri ali onse. Ndipo Davide anati kwa msonkhano wonse wa Israele, Chikakomera inu, ndipo chikachokera kwa Yehova Mulungu wathu, titumize konse kuti abale athu otsala m'dziko lonse la Israele, ndi ansembe ndi Alevi okhala nao m'midzi yao yokhala napo podyetsa, kuti asonkhane kwa ife; ndipo tibwere nalo kwa ife likasa la Mulungu wathu, pakuti sitinafunako masiku a Saulo. Ndipo a msonkhano onse anati kuti adzachita; pakuti chidayenera chinthuchi pamaso pa anthu onse. M'mwemo Davide anamemeza Aisraele onse kuyambira Sihori wa ku Ejipito mpaka polowera ku Hamati, kutenga likasa la Mulungu ku Kiriyati-Yearimu. Ndipo Davide ndi Aisraele onse pamodzi naye anakwera kunka ku Baala, ndiko ku Kiriyati-Yearimu wa m'Yuda, kukwera nalo kuchokera komweko likasa la Mulungu Yehova wakukhala pa akerubi, kumene aitanirako Dzina. Ndipo anatengera likasa la Mulungu pa galeta watsopano kuchokera kunyumba ya Abinadabu; ndi Uza ndi Ahiyo anayendetsa ng'ombe za pa galetayo. Ndipo Davide ndi Aisraele onse anasewera pamaso pa Mulungu ndi mphamvu yao yonse; ndi nyimbo, ndi azeze, ndi zisakasa, ndi malingaka, ndi nsanje, ndi malipenga. Ndipo pamene anafika ku dwale la Kidoni, Uza anatambasula dzanja lake kulichirikiza likasa, pakuti ng'ombe zikadapulumuka. Ndi mkwiyo wa Yehova unayakira Uza, namkantha, chifukwa anatambasulira likasa dzanja lake, nafa komweko pamaso pa Mulungu. Ndipo kudaipira Davide kuti Yehova adachita chipasulo ndi Uza; motero anatcha malowo Pereziuza, mpaka lero lino. Ndipo Davide anaopa Mulungu tsikulo, kuti, Ndidzafika nalo bwanji likasa la Mulungu kwathu? M'mwemo Davide sanafike nalo likasa kwao kumudzi wa Davide, koma analipambutsira kunyumba ya Obededomu wa ku Giti. Ndi likasa la Mulungu linakhala ndi banja la Obededomu m'nyumba mwake miyezi itatu; ndipo Yehova anadalitsa nyumba ya Obededomu, ndi zonse anali nazo. Ndipo Huramu mfumu ya Tiro anatumiza mithenga kwa Davide, ndi mikungudza, ndi amisiri omanga miyala, ndi amatabwa, kuti ammangire nyumba. Ndipo Davide anazindikira kuti Yehova adamkhazikitsa mfumu ya Israele; pakuti ufumu wake unakwezekadi, chifukwa cha anthu ake Israele. Ndipo Davide anatenga akazi ena ku Yerusalemu, nabala Davide ana aamuna ndi aakazi ena. Maina a ana anali nao m'Yerusalemu ndi awa: Samuwa, ndi Sobabu Natani, ndi Solomoni, ndi Ibara, ndi Elisuwa, ndi Elipeleti, ndi Noga, ndi Nefegi, ndi Yafiya, ndi Elisama, ndi Beeliyada, ndi Elifeleti. Pamene Afilisti anamva kuti anamdzoza Davide akhale mfumu ya Aisraele onse, Afilisti onse anakwera kufunafuna Davide; ndipo Davide anamva, nawatulukira. Afilisti tsono anafika, nafalikira m'chigwa cha Refaimu. Ndipo Davide anafunsira kwa Mulungu, kuti, Ndikwere kodi kuyambana ndi Afilisti? Mudzawapereka m'dzanja langa kodi? Ndipo Yehova anati kwa iye, Kwera, pakuti ndidzawapereka m'dzanja lako. Atafika tsono ku Baala-Perazimu, Davide anawakantha komweko; nati Davide, Mulungu anapasula adani anga ndi dzanja langa, ngati pokhamulira madzi. Chifukwa chake analitcha dzina la malowo Baala-Perazimu. Ndipo anasiyako milungu yao; nalamula Davide, ndipo anaitentha ndi moto. Ndipo Afilisti anabwerezanso, nafalikira m'chigwamo. Ndipo Davide anafunsiranso kwa Mulungu, nanena Mulungu naye, Usakwera kuwatsata, uwazungulire, nuwadzere pandunji pa mitengo ya mkandankhuku. Ndipo kudzali, pakumva iwe kuwayula kunsonga kwa mitengo ya mkandankhuku, pamenepo utulukire kunkhondo; pakuti Mulungu watulukira pamaso pako kukantha gulu la Afilisti. Nachita Davide monga Yehova adamuuza, nakantha gulu la Afilisti kuyambira ku Gibiyoni kufikira ku Gezere. Ndipo mbiri ya Davide inabuka m'maiko onse, nafikitsira Yehova kuopsa kwake pa amitundu onse. Ndipo Davide anadzimangira nyumba m'mudzi mwake, nakonzeratu malo likasa la Mulungu, naliutsira hema. Pamenepo Davide anati, Sayenera ena kusenza likasa la Mulungu koma Alevi ndiwo; pakuti Yehova anawasankha iwo kusenza likasa la Mulungu, ndi kumtumikira Iye kosatha. Ndipo Davide anasonkhanitsira Aisraele onse ku Yerusalemu, akwere nalo likasa la Yehova kumalo kwake adalikonzera. Ndipo Davide anasonkhanitsa ana a Aroni ndi Alevi; a ana a Kohati, Uriyele mkulu wao, ndi abale ake zana limodzi mphambu makumi awiri; a ana a Merari, Asaya mkulu wao, ndi abale ake mazana awiri mphambu makumi awiri; a ana a Geresomo, Yowele mkulu wao, ndi abale ake zana limodzi mphambu makumi atatu; a ana a Elizafani, Semaya mkulu wao, ndi abale ake mazana awiri; a ana a Hebroni, Eliyele mkulu wao, ndi abale ake makumi asanu ndi atatu; a ana a Uziyele, Aminadabu mkulu wao, ndi abale ake zana limodzi mphambu khumi ndi awiri. Ndipo Davide anaitana Zadoki ndi Abiyatara ansembe, ndi Alevi Uriyele, Asaya, ndi Yowele, Semaya, ndi Eliyele, ndi Aminadabu, nanena nao, Inu ndinu akulu a nyumba za makolo a Alevi, mudzipatule inu ndi abale anu omwe, kuti mukatenge ndi kukwera nalo likasa la Yehova Mulungu wa Israele ku malo ndalikonzera. Pakuti, chifukwa cha kusalinyamula inu poyamba paja, Yehova Mulungu wathu anachita chotipasula, popeza sitinamfunafuna Iye monga mwa chiweruzo. Momwemo ansembe ndi Alevi anadzipatula kuti akwere nalo likasa la Yehova Mulungu wa Israele. Ndipo ana a Alevi anasenza likasa la Mulungu pa mapewa ao, mphiko zili m'mwemo, monga Mose anawauza, monga mwa mau a Yehova. Ndipo Davide ananena ndi mkulu wa Alevi kuti aike abale ao oimbawo ndi zoimbira, zisakasa, ndi azeze, ndi nsanje, azimveketse ndi kukweza mau ao ndi chimwemwe. Ndipo Alevi anaika Hemani mwana wa Yowele, ndi a abale ake Asafu mwana wa Berekiya, ndi a ana a Merari, abale ao, Etani mwana wa Kusaya; ndi pamodzi nao abale ao a kulongosola kwachiwiri, Zekariya, Beni, ndi Yaaziele, ndi Semiramoti, ndi Yehiyele, ndi Uni, Eliyabu, ndi Benaya, ndi Maaseiya, ndi Matitiya, ndi Elifelehu, ndi Mikineya, ndi Obededomu, ndi Yeiyele, odikirawo. Oimba tsono: Hemani, Asafu, ndi Etani, anaimba ndi nsanje zamkuwa; ndi Zekariya, ndi Aziyele, ndi Semiramoti, ndi Yehiyele, ndi Uni, ndi Eliyabu, ndi Maaseiya, ndi Benaya, ndi zisakasa kuimbira mwa Alimoti; ndi Matitiya, ndi Elifelehu, ndi Mikineya, ndi Obededomu, ndi Yeiyele, ndi Azaziya, ndi azeze akuimbira mwa Seminiti, kutsogolera maimbidwe. Ndi Kenaniya mkulu wa Alevi anayang'anira kusenzako; anawalangiza za kusenza, pakuti anali waluso. Ndi Berekiya ndi Elikana anali odikira likasa. Ndi Sebaniya, ndi Yosafati, ndi Netanele, ndi Amasai, ndi Zekariya, ndi Benaya, ndi Eliyezere, ansembe, analiza malipenga ku likasa la Mulungu; ndi Obededomu ndi Yehiya anali odikira a likasa. Momwemo Davide, ndi akuluakulu a Israele, ndi atsogoleri a zikwi, anamuka kukwera nalo likasa la chipangano la Yehova, kuchokera kunyumba ya Obededomu mokondwera. Ndipo popeza Mulungu anathandiza Alevi akusenza likasa la chipangano la Yehova, iwo anapha nsembe ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri. Ndipo Davide anavala malaya abafuta, ndi Alevi onse akunyamula likasa, ndi oimba, ndi Kenaniya woyang'anira kusenzaku, pamodzi ndi oimba; Davide anavalanso efodi wabafuta. Momwemo Aisraele onse anakwera nalo likasa la chipangano la Yehova ndi kufuula, ndi kumveka kwa lipenga, ndi mphalasa, ndi nsanje zomveketsa, ndi zisakasa, ndi azeze. Ndipo polowa likasa la chipangano la Yehova m'mudzi wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Saulo anasuzumira pazenera, nao mfumu Davide alikutumphatumpha ndi kusewera; ndipo anampeputsa mumtima mwake. Ndipo analowa nalo likasa la Mulungu, naliika pakati pa hemalo Davide adaliutsira; ndipo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika pamaso pa Mulungu. Ndipo atatha Davide kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika, anadalitsa anthu m'dzina la Yehova. Nagwira aliyense wa Israele, wamwamuna ndi wamkazi, yense mtanda wa mkate, ndi nthuli ya nyama, ndi nchinchi ya mphesa zouma. Ndipo anaika Alevi ena atumikire ku likasa la Yehova, nalalikire, nayamike, nalemekeze Yehova Mulungu wa Israele. Asafu ndiye mkulu wao, ndi otsatana naye Zekariya, Yeiyele, ndi Semiramoti, ndi Yehiyele, ndi Matitiya, ndi Eliyabu, ndi Benaya, ndi Obededomu, ndi Yeiyele, ndi zisakasa ndi azeze; koma Asafu ndi nsanje zomvekatu; ndi Benaya ndi Yahaziele ansembe ndi malipenga kosalekeza, ku likasa la chipangano la Mulungu. Tsiku limenelo tsono Davide anayamba kuwapatsa nyimbo ya kuyamika nayo Yehova; ochita ndiwo Asafu ndi abale ake. Yamikani Yehova, itanani dzina lake; bukitsani mwa mitundu ya anthu zochita Iye. Muimbireni, muimbireni zomlemekeza; fotokozerani zodabwitsa zake zonse. Mudzitamandire ndi dzina lake lopatulika; mitima yao ya iwo ofuna Yehova ikondwere. Funsirani kwa Yehova ndi mphamvu yake; funani nkhope yake nthawi zonse. Kumbukirani zodabwitsa zake adazichita, zizindikiro zake, ndi maweruzo a pakamwa pake. Inu mbeu ya Israele mtumiki wake, inu ana a Yakobo, osankhika ake. Iye ndiye Yehova Mulungu wathu; maweruzo ake akhala pa dziko lonse lapansi. Kumbukirani chipangano chake kosatha, mauwo anawalamulira mibadwo zikwi; chipanganocho anapangana ndi Abrahamu, ndi lumbiro lake ndi Isaki; ndipo anachitsimikizira kwa Yakobo chikhale malemba, chikhale chipangano chosatha kwa Israele; ndi kunena kuti, Ndidzakupatsa iwe dziko la Kanani, gawo la cholandira chako. Pokhala inu anthu owerengeka, inde anthu pang'ono, ndi alendo m'mwemo; nayendayenda kuchokera mtundu wina kufikira mtundu wina, kuchokera ufumu wina kufikira anthu ena. Sanalole munthu awasautse; ndipo anadzudzula mafumu chifukwa cha iwowa; ndi kuti, Musamakhudza odzozedwa anga, musamachitira choipa aneneri anga. Muimbireni Yehova, inu dziko lonse lapansi, lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku. Fotokozerani ulemerero wake mwa amitundu, zodabwitsa zake mwa mitundu yonse ya anthu. Pakuti Yehova ali wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ayenera amuope koposa milungu yonse. Pakuti milungu ya mitundu ya anthu ndiyo mafano; koma Yehova analenga zakumwamba. Pamaso pake pali ulemu ndi ukulu, m'malo mwake muli mphamvu ndi chimwemwe. Mchitireni Yehova, inu mafuko a mitundu ya anthu, mchitireni Yehova ulemerero ndi mphamvu. Mchitireni Yehova ulemerero wa dzina lake; bwerani nacho chopereka, ndipo fikani pamaso pake; lambirani Yehova m'chiyero chokometsetsa. Njenjemerani pamaso pake, inu dziko lonse lapansi, dziko lokhalamo anthu lomwe lakhazikika, kuti silingagwedezeke. Kukondwerere kumwamba, ndi dziko lapansi lisekerere; anene mwa amitundu, Yehova achita ufumu. Nyanja ikukume m'kudzala kwake, munda ukondwerere, ndi zonse zili m'mwemo. Pamenepo mitengo yonse ya kunkhalango idzafuula mokondwera pamaso pa Yehova; pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi. Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino; pakuti chifundo chake nchosatha. Nimunene, Tipulumutseni, Mulungu wa chipulumutso chathu; mutisokolotse ndi kutilanditsa kwa amitundu, kuti tiyamike dzina lanu loyera, ndi kudzitamandira nacho chilemekezo chanu. Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israele, kuyambira kosayamba kufikira kosatha. Ndipo anthu onse anati, Amen! Nalemekeza Yehova. Ndipo anasiyako ku likasa la chipangano la Yehova Asafu ndi abale ake, atumikire kulikasa kosalekeza, monga umo mudzafunika tsiku ndi tsiku; ndi Obededomu, ndi abale ake makumi asanu ndi limodzi mphambu asanu ndi atatu; ndi Obededomu mwana wa Yedutuni ndi Hosa akhale odikira; ndi Zadoki wansembe, ndi abale ake ansembe, ku Kachisi wa Yehova, pa msanje unali ku Gibiyoni; kupereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa guwa la nsembe zopsereza, kosalekeza, m'mawa ndi madzulo, monga mwa zonse zilembedwa m'chilamulo cha Yehova adachilamulira Israele; ndi pamodzi nao Hemani, ndi Yedutuni, ndi osankhika otsalawo, otchulidwa maina, kuyamika Yehova; pakuti chifundo chake nchosatha; ndi pamodzi nao Hemani, ndi Yedutuni, ndi malipenga ndi nsanje za iwo akumveketsadi, ndi zoimbira nyimbo za Mulungu; ndi ana a Yedutuni anakhala kuchipata. Ndipo anachoka anthu onse, yense kunyumba yake, nabwera Davide kudalitsa nyumba yake. Ndipo pokhala Davide m'nyumba mwake, Davideyo anati kwa Natani mneneri, Taona, ndikhala ine m'nyumba yamikungudza, koma likasa la chipangano la Yehova likhala m'nsalu zotchinga. Ndipo Natani anati kwa Davide, Muchite zonse zili m'mtima mwanu; pakuti Mulungu ali nanu. Ndipo usiku womwewo mau a Mulungu anadzera Natani, ndi kuti, Kauze Davide mtumiki wanga, Atero Yehova, Usandimangire nyumba yokhalamo; pakuti sindinakhala m'nyumba kuyambira tsiku lija ndinakwera naye Israele, kufikira lero lino; koma ndakhala ndikuyenda m'mahema uku ndi uku. Pali ponse ndinayenda nao Aisraele onse ndinanena kodi mau ndi woweruza aliyense wa Israele, amene ndinamuuza adyetse anthu anga, ndi kuti, Mwalekeranji kundimangira nyumba yamikungudza? Chifukwa chake tsono, uzitero naye mtumiki wanga Davide, Atero Ambuye wa makamu, Ndinakutenga kubusa potsata iwe nkhosa, kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Israele; ndipo ndakhala ndi iwe kulikonse unamukako, ndi kuononga adani ako onse pamaso pako; ndipo ndakubukitsira dzina lakunga dzina la akulu okhala padziko. Ndipo ndaikira anthu anga Israele malo, ndi kuwaoka, kuti akhale m'malo mwao osasunthikanso; ndi ana osalungama sadzawapululanso monga poyamba paja; ndi kuyambira kuja ndinaika oweruza ayang'anire anthu anga Israele; ndipo ndagonjetsa adani ako onse. Ndikuuzanso kuti Yehova adzakumangira banja. Ndipo kudzachitika, atakwanira masiku ako kuti uzipita kukhala ndi makolo ako, ndidzaukitsa mbeu yako pambuyo pako, ndiye wa ana ako; ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake. Iye adzandimangira nyumba; ndipo ndidzakhazikitsa mpando wachifumu wake kosatha. Ndidzakhala atate wake, ndi iye adzakhala mwana wanga; ndipo sindidzamchotsera chifundo changa monga muja ndinachotsera iye amene anakhala usanakhale iwe; koma ndidzamkhazikitsa m'nyumba mwanga, ndi m'ufumu wanga kosatha; ndi mpando wa chifumu wake udzakhazikika kosatha. Monga mwa mau awa onse, ndi monga mwa masomphenya awa onse, momwemo Natani analankhula ndi Davide. Pamenepo mfumu Davide analowa nakhala pamaso pa Yehova, nati, Ndine yani, Yehova Mulungu, ndi nyumba yanga njotani kuti mwandifikitsa mpaka pano? Ndipo ichi nchaching'ono pamaso panu, Mulungu, koma mwanena za nyumba ya mtumiki wanu nthawi yam'tsogolo ndithu, ndipo mwandiyesera ngati munthu womveka, Yehova Mulungu. Anenenjinso Davide kwa inu za ulemu wochitikira mtumiki wanu? Pakuti mudziwa mtumiki wanu. Yehova, chifukwa cha mtumiki wanu, ndi monga mwa mtima wanu, mwachita ukulu uwu wonse, kundidziwitsa zazikulu izi zonse. Yehova, palibe wina wonga inu, palibenso Mulungu wina koma Inu; monga mwa zonse tazimva m'makutu mwathu. Ndiwo ayani akunga anthu anu Israele, mtundu wa pa wokha wa pa dziko lapansi, amene Mulungu anakadziombolera mtundu wa anthu, kudzibukitsira dzina, mwa zazikulu ndi zoopsa, pakupirikitsa amitundu pamaso pa anthu anu amene munawaombola m'Ejipito? Pakuti anthu anu Israele mudawayesa anthu anuanu kosatha; ndipo Inu, Yehova, munayamba kukhala Mulungu wao. Ndipo tsopano, Yehova, akhazikike kosalekeza mau mudanenawa za mtumiki wanu, ndi za nyumba yake, nimuchite monga mwanena. Inde likhazikike dzina lanu, likulitsidwe kosalekeza, ndi kuti, Yehova wa makamu ndiye Mulungu wa Israele; akhalira Israele Mulungu; ndi nyumba ya Davide mtumiki wanu ikhazikika pamaso panu. Pakuti Inu, Mulungu wanga, mwaululira mtumiki wanu kuti mudzammangira banja; momwemo mtumiki wanu waona mtima wakupemphera pamaso panu. Ndipo tsopano, Yehova, Inu ndinu Mulungu, ndipo mwanenera mtumiki wanu chokoma ichi; chakukomerani kudalitsa nyumba ya mtumiki wanu, kuti ikhalebe kosatha pamaso panu; pakuti Inu Yehova mwadalitsa, ndipo idzadalitsika kosatha. Ndipo zitatha izi, Davide anakantha Afilisti, nawagonjetsa, nalanda Gati ndi midzi yake m'manja a Afilisti. Anakanthanso Mowabu; ndi Amowabu anakhala anthu a Davide, nabwera nazo mphatso. Ndipo Davide anakantha Hadadezere mfumu ya Zoba ku Hamati, pomuka iye kukhazikitsa ulamuliro wake ku mtsinje wa Yufurate. Ndipo Davide analanda magaleta ake chikwi chimodzi, ndi apakavalo zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi oyenda pansi zikwi makumi awiri; Davide anadula mitsita akavalo onse okoka magaleta, koma anasungako ofikira magaleta zana limodzi. Ndipo Aaramu a ku Damasiko anadza kudzathandiza Hadadezere mfumu ya Zoba; koma Davide anakantha Aaramu amuna zikwi makumi awiri mphambu ziwiri. Ndipo Davide anaika asilikali a boma m'Aramu wa Damasiko; ndi Aaramu anasanduka anthu a Davide, nabwera nazo mphatso. Ndipo Yehova anasunga Davide kulikonse anamukako. Natenga Davide zikopa zagolide zinali pa anyamata a Hadadezere, nabwera nazo ku Yerusalemu. Ndi ku Tibati, ndi ku Kuni, midzi ya Hadadezere, Davide anatenga mkuwa wambiri, ndiwo umene Solomoni anayenga nao thawale lamkuwa, ndi nsanamira, ndi zipangizo zamkuwa. Ndipo pakumva Tou, mfumu ya ku Hamati, kuti Davide adakantha khamu lonse la Hadadezere mfumu ya ku Zoba, anatumiza Hadoramu mwana wake kwa mfumu Davide, kumlonjera ndi kumdalitsa, popeza adayambana ndi Hadadezere, namkantha; pakuti Hadadezere adachita nkhondo ndi Tou; ndipo anali nazo zipangizo za mitundumitundu za golide ndi siliva ndi mkuwa. Izi zomwe mfumu Davide anazipatulira Yehova, pamodzi ndi siliva ndi golide adazitenga kwa amitundu onse, kwa Edomu, ndi kwa Mowabu, ndi kwa ana a Amoni, ndi kwa Afilisti, ndi kwa Amaleke. Ndipo Abisai mwana wa Zeruya anakantha Aedomu m'Chigwa cha Mchere zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu. Ndipo anaika asilikali a boma m'Edomu; ndi Aedomu onse anasanduka anthu a Davide. Ndipo Yehova anasunga Davide kulikonse anamukako. Ndipo Davide anakhala mfumu ya Aisraele onse, naweruza anthu ake onse, nawachitira chilungamo. Ndipo Yowabu mwana wa Zeruya anayang'anira khamu la nkhondo, ndi Yehosafati mwana wa Ahiludi anali wolemba mbiri. Ndi Zadoki mwana wa Ahitubi, ndi Ahimeleki mwana wa Abiyatara, anali ansembe, ndi Savisa anali mlembi, ndi Benaya mwana wa Yehoyada anayang'anira Akereti ndi Apeleti; koma ana a Davide ndiwo oyamba ku dzanja la mfumu. Ndipo zitatha izi, Nahasi mfumu ya ana a Amoni anamwalira, ndi mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake. Ndipo Davide anati, Ndidzamchitira zokoma mtima Hanuni mwana wa Nahasi, popeza atate wake anandichitira ine zokoma mtima. Momwemo Davide anatuma mithenga imtonthoze mtima pa atate wake. Pofika anyamata ake a Davide ku dziko la ana a Amoni kwa Hanuni kumtonthoza mtima, akalonga a ana a Amoni anati kwa Hanuni, Davide ali kuchitira atate wanu ulemu kodi, popeza anakutumizirani otonthoza? Sakudzerani kodi anyamata ake kufunafuna, ndi kugubuduza, ndi kuzonda dziko? Ndipo Hanuni anatenga anyamata a Davide, nawameta, nadula malaya ao pakati kufikira m'matako, nawaleka achoke. Pamenepo anamuka ena namuuza Davide za amunawa. Natumiza iye kukomana nao, pakuti amunawa anachita manyazi kwambiri. Ndipo mfumu inati, Balindani ku Yeriko mpaka zamera ndevu zanu; zitamera mubwere. Ndipo pamene ana a Amoni anaona kuti anadzinunkhitsa kwa Davide, Hanuni ndi ana a Amoni anatumiza matalente chikwi chimodzi a siliva, kudzilembera magaleta ndi apakavalo ku Mesopotamiya, ndi ku Aramu-Maaka, ndi ku Zoba. Momwemo anadzilembera magaleta zikwi makumi atatu mphambu ziwiri, ndi mfumu ya Maaka ndi anthu ake; nadza iwo, namanga misasa chakuno cha Medeba. Ana a Amoni omwe anasonkhana m'midzi mwao, nadza kunkhondo. Pamene Davide anamva ichi anatuma Yowabu ndi gulu lonse la anthu amphamvu. Ndipo ana a Amoni anatuluka, nandandalitsa nkhondo ku chipata cha mudzi, ndi mafumu adadzawo anali pa okha kuthengo. Pakuona Yowabu tsono kuti nkhondo inamdzera kumaso ndi kumbuyo, anasankha amuna osankhika onse a Israele, nawanika ayambane ndi Aaramu. Ndipo anthu otsala anawapereka m'dzanja la Abisai mbale wake; ndipo anadzinika ayambane ndi ana a Amoni. Ndipo anati, Akandiposa mphamvu Aaramu, udzandilanditsa ndiwe; koma akakuposa mphamvu ana a Amoni, ndidzakulanditsa ndine. Limbika mtima, tilimbikire anthu athu, ndi midzi ya Mulungu wathu; ndipo Yehova achite chomkomera. Pamenepo Yowabu ndi anthu anali naye anayandikira pamaso pa Aaramu kulimbana nao, ndipo anawathawa. Ndipo pakuona ana a Amoni kuti adathawa Aaramu, iwo omwe anathawa pamaso pa Abisai mbale wake, nalowa m'mudzi. Pamenepo Yowabu anadza ku Yerusalemu. Ndipo pakuona Aaramu kuti Israele anawakantha, anatumiza mithenga, natuluka nao Aaramu akukhala tsidya lija la mtsinjewo; ndi Sofaki kazembe wa khamu la Hadadezere anawatsogolera. Ndipo anamuuza Davide; namemeza iye Aisraele onse, naoloka Yordani, nawadzera, nanika nkhondo ayambane nao. Atandandalitsa nkhondo Davide kuyambana ndi Aaramu, anaponyana naye. Ndipo Aaramu anathawa pamaso pa Israele; ndipo Davide anapha Aaramu apamagaleta zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi oyenda pansi zikwi makumi anai; napha Sofaki kazembe wa khamulo. Ndipo pakuona anyamata a Hadadezere kuti Israele anawakantha, anapangana mtendere ndi Davide, namtumikira; ndi Aaramu anakana kuthandizanso ana a Amoni. Ndipo kunali, pofikanso chaka, nyengo yakutuluka mafumu, Yowabu anatsogolera khamu lamphamvu, napasula dziko la ana a Amoni, nadza, naumangira misasa Raba. Koma Davide anakhala ku Yerusalemu. Ndipo Yowabu anakantha Raba, naupasula. Ndipo Davide anatenga korona wa mfumu yao kumchotsa pamutu pake, napeza kulemera kwake talente wa golide; panalinso miyala ya mtengo wake pamenepo; ndipo anamuika pamutu pa Davide, natulutsa zankhondo za m'mudzimo zambiri ndithu. Natulutsanso anthu anali m'mwemo, nawacheka ndi mipeni ya manomano, ndi zipangizo zochekera zachitsulo, ndi nkhwangwa. Anatero Davide ndi midzi yonse ya ana a Amoni. Ndipo Davide ndi anthu onse anabwera ku Yerusalemu. Ndipo zitatha izi, inauka nkhondo ku Gezere ndi Afilisti; pamenepo Sibekai Muhusa anapha Sipai wa ana a chimphona; ndipo anawagonjetsa. Ndipo panalinso nkhondo ndi Afilisti; ndi Elihanani mwana wa Yairi anapha Lami mbale wa Goliyati Mgiti, amene luti la mkondo wake linanga mtanda woombera nsalu. Ndipo panalinso nkhondo ku Gati; kumeneko kunali munthu wa msinkhu waukulu, amene zala zake za kumanja ndi kumapazi ndizo makumi awiri mphambu zinai; zisanu ndi chimodzi ku dzanja lililonse, ndi zisanu ndi chimodzi ku phazi lililonse; nayenso anabadwa mwa chimphonacho. Ndipo potonza Israele iyeyu Yonatani mwana wa Simea mbale wake wa Davide anamkantha. Awa anabadwa mwa chimphonacho ku Gati, koma anagwa ndi dzanja la Davide ndi la anyamata ake. Pamenepo Satana anaukira Israele, nasonkhezera Davide awerenge Israele. Ndipo Davide anati kwa Yowabu ndi kwa akulu a anthu, Kawerengeni Israele kuyambira ku Beereseba kufikira ku Dani; nimundibwezere mau, kuti ndidziwe chiwerengo chao. Nati Yowabu, Yehova aonjezere pa anthu ake monga ali kazana; koma, mbuyanga mfumu, sali onse anyamata akapolo a mbuyanga? Nanga afuniranji chinthuchi mbuyanga, adzapalamulitsa Israele bwanji? Koma mau a mfumu anamlaka Yowabu. Natuluka Yowabu, nakayendayenda mwa Aisraele onse, nadza ku Yerusalemu. Ndipo Yowabu anapereka kwa Davide chiwerengo cha anthu owerengedwa. Ndipo Aisraele onse anali zikwi mazana khumi ndi limodzi osolola lupanga, ndi Yuda anali zikwi mazana anai mphambu makumi asanu ndi awiri akusolola lupanga. Koma sanawerenge Alevi ndi Abenjamini pakati pao; pakuti mau a mfumu anamnyansira Yowabu. Ndipo Mulungu anaipidwa nacho chinthuchi, chifukwa chake Iye anakantha Israele. Pamenepo Davide anati kwa Mulungu, Ndachimwa kwakukulu ndi kuchita chinthu ichi; koma tsopano, muchotse mphulupulu ya kapolo wanu, pakuti ndachita kopusa ndithu. Ndipo Yehova ananena ndi Gadi mlauli wa Davide, ndi kuti, Kanene kwa Davide kuti, Atero Yehova, Ndikuikira zitatu; dzisankhireko chimodzi ndikuchitire ichi. Nadza Gadi kwa Davide, nanena naye, Atero Yehova, Dzitengereko; kapena zaka zitatu za njala; kapena miyezi itatu ya kuthedwa pamaso pa adani ako, ndi kuti lupanga la adani ako likupeze; kapena masiku atatu lupanga la Yehova, ndilo mliri m'dzikomo, ndi mthenga wakuononga wa Yehova mwa malire onse a Israele. Ulingirire tsono, ndimbwezere mau anji Iye amene anandituma ine? Ndipo Davide anati kwa Gadi, Ndipsinjika kwambiri; ndigwere m'dzanja la Yehova, pakuti zifundo zake zichulukadi; koma ndisagwere m'dzanja la munthu. Momwemo Yehova anatumiza mliri pa Israele; ndipo adagwapo amuna zikwi makumi asanu ndi awiri a Israele. Ndipo Mulungu anatuma mthenga ku Yerusalemu kuuononga; ndipo poti auononge, Yehova anapenya, naleka choipachi; nati kwa mthenga wakuononga, Chakwanira, bweza dzanja lako tsopano. Ndi mthenga wa Yehova anaima pa dwale la Orinani Myebusi. Ndipo Davide anakweza maso ake, naona mthenga wa Yehova alikuima pakati pa dziko ndi thambo, ali nalo lupanga losolola m'dzanja lake, lotambasukira pa Yerusalemu. Pamenepo Davide ndi akulu ovala ziguduli anagwa nkhope zao pansi. Ndipo Davide anati kwa Mulungu, Si ndine nanga ndalamulira kuti awerenge anthu? Inde, ndine amene ndachimwa ndi kuchita choipa ndithu; koma nkhosa izi zinachitanji? Dzanja lanu, Yehova Mulungu wanga, linditsutse ine ndi nyumba ya atate wanga, koma lisatsutse anthu anu ndi kuwachitira mliri. Pamenepo mthenga wa Yehova anauza Gadi kuti anene ndi Davide, akwere Davideyo kuutsira Yehova guwa la nsembe pa dwale la Orinani Myebusi. Ndipo Davide anakwera monga mwa mau a Gadi adawanena m'dzina la Yehova. Pocheuka Orinani anaona wamthengayo; ndi ana ake amuna anai anali naye anabisala. Koma Orinani analikupuntha tirigu. Ndipo pofika Davide kwa Orinani, Orinaniyo anapenyetsa, naona Davide, natuluka kudwale, nawerama kwa Davide, nkhope yake pansi. Davide tsono anati kwa Orinani, Ndipatse padwale pano kuti ndimangepo guwa la nsembe la Yehova; undipatse ili pa mtengo wake wonse, kuti mliri ulekeke pa anthu. Ndipo Orinani anati kwa Davide, Mulitenge, ndi mbuye wanga mfumu ichite chomkomera m'maso mwake; taonani, ndikupatsani ng'ombe za nsembe zopsereza; ndi zipangizo zopunthira zikhale nkhuni, ndi tirigu wa nsembe yaufa; ndizipereka zonse. Koma mfumu Davide anati kwa Orinani, Iai, koma ndidzaligula pa mtengo wake wonse; pakuti sindidzatengera Yehova chili chako, kapena kupereka nsembe yopsereza yopanda mtengo wake. Momwemo Davide anapatsa Orinani chogulira malowa golide wa masekeli mazana asanu ndi limodzi kulemera kwake. Ndipo Davide anamangira Yehova guwa la nsembe komweko; napereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika, naitana kwa Yehova; ndipo anamyankha ali m'Mwamba ndi moto pa guwa la nsembe yopsereza. Ndipo Yehova anauza wamthenga kuti abweze lupanga lake m'chimake. Nthawi yomweyi, pakuona Davide kuti Yehova anamvomereza pa dwale la Orinani Myebusi, anaphera nsembe pomwepo. Pakuti Kachisi wa Yehova amene Mose anapanga m'chipululu, ndi guwa la nsembe yopsereza, zinali pa msanje wa ku Gibiyoni nthawi yomweyi. Koma Davide sanathe kumuka kukhomo kwake kufunsira kwa Mulungu, pakuti anaopa lupanga la mthenga wa Yehova. Ndipo Davide anati, Pano padzakhala nyumba ya Yehova Mulungu, ndi pano padzakhala guwa la nsembe yopsereza la Israele. Ndipo Davide anati asonkhanitse alendo okhala m'dziko la Israele; iye naika osema miyala afukule miyala, aiseme kuti amange nayo nyumba ya Mulungu. Nakonzeratu Davide chitsulo chochuluka cha misomali ya ku zitseko za zipata, ndi ya kuphatikizitsa; ndi mkuwa wochuluka wosauyesa kulemera kwake; ndi mitengo yamikungudza yosaiwerenga; pakuti Asidoni ndi Atiro anabwera nayo kwa Davide mitengo yamikungudza yochuluka. Ndipo Davide anati, Solomoni mwana wanga ndiye mnyamata ndi wosakwima, ndi nyumba imene adzaimangira Yehova ikhale yaikulu yopambana, yomveka ndi ya ulemerero mwa maiko onse; ndiikonzeretu mirimo. Momwemo Davide anakonzeratu mochuluka asanamwalire. Pamenepo iye anaitana Solomoni mwana wake, namlangiza ammangire Yehova Mulungu wa Israele nyumba. Ndipo Davide anati kwa Solomoni mwana wake, Kunena za ine, kumtima kwanga kudati, ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba. Koma mau a Yehova anandidzera, kuti, Wakhetsa mwazi wochuluka, popeza wachita nkhondo zazikulu; sudzamangira dzina langa nyumba, popeza wakhetsa pansi mwazi wambiri pamaso panga; taona, udzabala mwana, ndiye adzakhala munthu wa phee; ndipo ndidzampumulitsira adani ake onse pozungulirapo, pakuti dzina lake lidzakhala Solomoni; ndipo ndidzapatsa Israele mtendere ndi bata masiku ake; iyeyu adzamangira dzina langa nyumba; iye adzakhala mwana wanga, ndi Ine ndidzakhala Atate wake; ndipo ndidzakhazikitsa mpando wachifumu wa ufumu wake pa Israele, kosalekeza. Tsono, mwana wanga, Yehova akhale nawe; nulemerere, numange nyumba ya Yehova Mulungu wako monga ananena za iwe. Chokhachi, Yehova akupatse nzeru ndi luntha, nakulangize za Israele, kuti usunge chilamulo cha Yehova Mulungu wako. Momwemo udzalemerera, ukasamalira kuchita malemba ndi maweruzo amene Yehova analangiza Mose za Israele; limbikatu, nulimbike mtima, usaope, usade mtima. Taona tsono, m'kuzunzika kwanga ndinakonzeratu nyumba ya Yehova matalente zikwi zana limodzi a golide, ndi matalente zikwizikwi a siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, osayesa kulemera kwake, pakuti zidachulukadi; mitengo yomwe ndi miyala ndakonzeratu; nuonjezereko. Uli naonso antchito ochuluka ofukula miyala, ndi amisiri a miyala ndi a mitengo, ndi amuna onse aluso akuchita ntchito zilizonse; golide, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, nzosawerengeka; nyamuka, nuchite, Yehova akhale nawe. Davide analangizanso akalonga a Israele athandize Solomoni mwana wake, ndi kuti, Kodi Yehova Mulungu wanu sali nanu? Sanakupumulitseni pambali ponse? Pakuti anapereka nzika za m'dziko m'dzanja mwanga, ndi dziko lagonjetsedwa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa anthu ake. Perekani tsono mtima ndi moyo wanu kufunafuna Yehova Mulungu wanu; ndipo nyamukani ndi kumanga malo opatulika a Yehova Mulungu, kuti abwere nalo likasa la chipangano la Yehova, ndi zipangizo zopatulika za Mulungu, kunyumba imene idzamangidwira dzina la Yehova. Atakalamba tsono Davide ndi kuchuluka masiku, iye analonga mwana wake Solomoni akhale mfumu ya Israele. Ndipo anasonkhanitsa akulu onse a Israele, ndi ansembe ndi Alevi. Ndipo anawerengedwa Alevi oyambira zaka makumi atatu ndi mphambu, ndipo chiwerengo chao kuwawerenga mmodzimmodzi ndicho amuna zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu. A iwowa zikwi makumi awiri mphambu zinai anayang'anira ntchito ya nyumba ya Yehova, ndi zikwi zisanu ndi chimodzi ndiwo akapitao ndi oweruza, ndi zikwi zinai odikira; ndi zikwi zinai analemekeza Yehova ndi zoimbira zimene ndinazipanga, anati Davide, kuti alemekeze nazo. Ndipo Davide anawagawa magawo monga mwa ana a Levi: Geresoni, Kohati, ndi Merari. A Ageresoni: Ladani ndi Simei. Ana a Ladani: wamkulu ndi Yehiyele, ndi Zetamu, ndi Yowele; atatu. Ana a Simei: Selomoti, ndi Haziyele, ndi Harani; atatu. Ndiwo akulu a nyumba za makolo a Ladani. Ndi ana a Simei: Yahati, Zina, ndi Yeusi, ndi Beriya. Awa anai ndiwo ana a Simei. Wamkulu wa iwo ndi Yahati, mnzake ndi Ziza; koma Yeusi ndi Beriya analibe ana ambiri, potero anakhala nyumba ya kholo yowerengedwa pamodzi. Ana a Kohati: Amuramu, Izihara, Hebroni, ndi Uziyele; anai. Ana a Amuramu: Aroni, ndi Mose; ndipo Aroni anasankhidwa kuti apatule zopatulika kwambiri, iye ndi ana ake, kosalekeza, kufukiza pamaso pa Yehova, kumtumikira, ndi kudalitsa m'dzina lake kosatha. Kunena za Mose munthu wa Mulunguyo, ana ake anatchulidwa mwa fuko la Levi. Ana a Mose: Geresomo, ndi Eliyezere. Ana a Geresomo: wamkulu ndi Sebuele. Ndi ana a Eliyezere: wamkulu ndi Rehabiya. Ndipo Eliyezere analibe ana ena, koma ana a Rehabiya anachuluka kwambiri. Ana a Izihara: wamkulu ndiye Selomiti. Ana a Hebroni: wamkulu ndi Yeriya, wachiwiri ndi Amariya, wachitatu ndi Yahaziele, wachinai ndi Yekameamu. Ana a Uziyele: wamkulu ndi Mika, wachiwiri ndi Isiya. Ana a Merari: Mali ndi Musi. Ndi ana a Mali: Eleazara ndi Kisi. Nafa Eleazara wopanda ana amuna, koma ana akazi ndiwo; ndi asuweni ao ana a Kisi anawatenga akhale akazi ai. Ana a Musi: Mali, ndi Edere, ndi Yeremoti; atatu. Awa ndi ana a Levi monga mwa nyumba za makolo ao, ndiwo akulu a nyumba za makolo a iwo owerengedwa mwa chiwerengero cha maina mmodzimmodzi, akugwira ntchito ya utumiki wa nyumba ya Yehova, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu. Pakuti Davide anati, Yehova Mulungu wa Israele wapumulitsa anthu ake; ndipo akhala m'Yerusalemu kosatha; ndiponso Alevi asasenzenso Kachisi ndi zipangizo zake zonse za utumiki wake. Pakuti monga mwa mau ake otsiriza a Davide, ana a Levi anawerengedwa kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu. Pakuti ntchito yao ndiyo kuimirira ana a Aroni, atumikire m'nyumba ya Yehova, m'mabwalo, ndi kuzipinda, ndi kuyeretsa zopatulika zonse; inde ntchito za utumiki wa nyumba ya Mulungu; ya mkate woonekera womwe, ndi ya ufa wosalala wa nsembe yaufa, ndi ya timitanda taphanthiphanthi topanda chotupitsa, ndi ya chiwaya, ndi yakukazinga, ndi ya miyeso iliyonse; ndi kuimirira m'mawa ndi m'mawa kuyamika ndi kulemekeza Yehova, momwemonso madzulo; ndi kupereka nsembe zopsereza zonse kwa Yehova, za masabata, za pokhala mwezi, za nyengo zoikika, kuwerenga kwake monga mwa lemba lake, kosalekeza pamaso pa Yehova; ndi kuti asunge udikiro wa chihema chokomanako, ndi udikiro wa malo opatulika ndi udikiro wa ana a Aroni abale ao, potumikira nyumba ya Yehova. Ndipo magawidwe a ana a Aroni ndi awa. Ana a Aroni: Nadabu, ndi Abihu, Eleazara, ndi Itamara. Koma Nadabu ndi Abihu anafa, atate wao akali ndi moyo, opanda ana; momwemo Eleazara ndi Itamara anachita ntchito ya nsembe. Ndipo Davide pamodzi ndi Zadoki wa ana a Eleazara, ndi Ahimeleki wa ana a Itamara, anawagawa, monga mwa malongosoledwe ao m'utumiki wao. Ndipo anapeza kuti amuna akulu a ana a Eleazara anachuluka, a ana a Itamara anachepa; nawagawa motero: pa ana a Eleazara panali khumi mphambu asanu ndi mmodzi, akulu a nyumba za makolo; ndi pa ana a Itamara, monga mwa nyumba za makolo ao, panali asanu ndi atatu. Ndipo anawagawa ndi maere, awa ndi aja; pakuti panali akalonga a malo opatulika, ndi akalonga a kwa Mulungu, a ana a Eleazara ndi a ana a Itamara omwe. Ndi Semaya mwana wa Netanele mlembi, ndiye wa Alevi, anawalembera pamaso pa mfumu; ndi akalonga, ndi Zadoki wansembe, ndi Ahimeleki mwana wa Abiyatara, a akulu a nyumba za makolo a ansembe ndi Alevi, anatenga nyumba imodzi ya kholo lake ya Eleazara, ndi imodzi ya Itamara. Ndipo maere oyamba anamgwera Yehoyaribu, wachiwiri Yedaya, wachitatu Harimu, wachinai Seorimu, wachisanu Malikiya, wachisanu ndi chimodzi Miyamini, wachisanu ndi chiwiri Hakozi, wachisanu ndi chitatu Abiya, wachisanu ndi chinai Yesuwa, wakhumi Sekaniya, wakhumi ndi chimodzi Eliyasibu, wakhumi ndi chiwiri Yakimu, wakhumi ndi chitatu Hupa, wakhumi ndi chinai Yesebeabu, wakhumi ndi chisanu Biliga, wakhumi ndi chisanu ndi chimodzi Imeri, wakhumi ndi chisanu ndi chiwiri Heziri, wakhumi ndi chisanu ndi chitatu Hapizeze, wakhumi ndi chisanu ndi chinai Petahiya, wa makumi awiri Yehezikele, wa makumi awiri ndi chimodzi Yakini, wa makumi awiri ndi chiwiri Gamuli, wa makumi awiri ndi chitatu Delaya, wa makumi awiri ndi chinai Maaziya. Awa ndi malongosoledwe ao m'utumiki wao kulowa m'nyumba ya Yehova, monga mwa chiweruzo adawapatsa Aroni atate wao, monga Yehova Mulungu wa Israele anamlamulira. Ndipo wa ana otsala a Levi: wa ana a Amuramu, Subaele; wa ana a Subaele, Yedeiya. Wa Rehabiya: wa ana a Rehabiya, mkulu ndi Isiya. Wa Aizihara: Selomoti; wa ana a Selomoti, Yahati. Ndi wa ana a Hebroni: mkulu ndi Yeriya, wachiwiri Amariya, wachitatu Yahaziele, wachinai Yekameamu. Wa ana a Uziyele, Mika; wa ana a Mika, Samiri. Mbale wa Mika, Isiya; a ana a Isiya, Zekariya. Ana a Merari: Mali ndi Musi; mwana wa Yaziya, Beno. Ana a Merari: wa Yaziya, Beno, ndi Sohamu, ndi Zakuri, ndi Ibiri. Wa Mali: Eleazara, ndiye wopanda ana. Wa Kisi: mwana wa Kisi, Yerameele. Ndi ana a Musi: Mali, ndi Edere, ndi Yerimoti. Awa ndi ana a Alevi monga mwa nyumba za makolo ao. Awanso anachita maere monga abale ao ana a Aroni, pamaso pa Davide mfumu, ndi Zadoki, ndi Ahimeleki, ndi akulu a nyumba za makolo za ansembe ndi Alevi; mkulu wa nyumba za makolo monga mng'ono wake. Ndipo Davide ndi akazembe a gulu la nkhondo anapatulira utumikiwo ena a ana a Asafu, ndi a Hemani, ndi a Yedutuni, anenere ndi azeze, ndi zisakasa, ndi nsanje; ndi chiwerengo cha antchito monga mwa kutumikira kwao ndicho: a ana a Asafu: Zakuri, ndi Yosefe, ndi Netaniya, ndi Asarela, ana a Asafu; mwa chilangizo cha Asafu, wakunenera mwa chilangizo cha mfumu. A Yedutuni, ana a Yedutuni: Gedaliya, ndi Zeri, ndi Yesaya, Hasabiya, ndi Matitiya, asanu ndi mmodzi; mwa chilangizo cha atate wao Yedutuni, ndiye wakunenera ndi kuyamika ndi kulemeza Yehova ndi zeze. A Hemani, ana a Hemani: Bukiya, Mataniya, Uziyele, Sebuele, ndi Yerimoti, Hananiya, Hanani, Eliyata, Gidaliti, ndi Romamiti-Ezere, Yosibekasa, Maloti, Hotiri, Mahaziyoti; awa onse ndiwo ana a Hemani mlauli wa mfumu m'mau a Mulungu, kuti akweze mphamvu yake. Ndipo Mulungu anapatsa Hemani ana amuna khumi ndi anai, ndi ana akazi atatu. Onsewa anawalangiza ndi atate wao aimbe m'nyumba ya Yehova ndi nsanje, zisakasa ndi azeze; atumikire nazo m'nyumba ya Mulungu; ndipo Asafu, Yedutuni, ndi Hemani, anawalangiza ndi mfumu. Ndipo chiwerengo chao, pamodzi ndi abale ao ophunzitsidwa aimbire Yehova, onse anthetemya, ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu. Ndipo anachita maere pa udikiro wao, analingana onse, ang'ono ndi akulu, mphunzitsi ndi wophunzira. Maere oyamba tsono anagwera a banja la Asafu ndiye Yosefe; wachiwiri Gedaliya, iye ndi abale ake, ndi ana ake khumi ndi awiri; wachitatu Zakuri, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri; wachinai Iziri, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri; wachisanu Netaniya, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri; wachisanu ndi chimodzi Bukiya, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri; wachisanu ndi chiwiri Yesarela, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri; wachisanu ndi chitatu Yesaya, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri; wachisanu ndi chinai Mataniya, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri; wakhumi Simei, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri; wakhumi ndi chimodzi Azarele, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri; wakhumi ndi chiwiri Hasabiya, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri; wakhumi ndi chitatu Subaele, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri; wakhumi ndi chinai Matitiya, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri; wakhumi ndi chisanu Yeremoti, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri; wakhumi ndi chisanu ndi chimodzi Hananiya, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri; wakhumi ndi chisanu ndi chiwiri Yosibekasa, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri; wakhumi ndi chisanu ndi chitatu Hanani, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri; wakhumi ndi chisanu ndi chinai Maloti, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri; wamakumi awiri Eliyata, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri; wa makumi awiri ndi chimodzi Hotiri, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri; wa makumi awiri ndi chiwiri Gidaliti, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri; wa makumi awiri ndi chitatu Mahaziyoti, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri; wa makumi awiri ndi chinai Romamiti-Ezere, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri. A magawidwe a odikira a Akora: Meselemiya mwana wa Kore wa ana a Asafu. Ndipo Meselemiya anali ndi ana, woyamba Zekariya, wachiwiri Yediyaele, wachitatu Zebadiya, wachinai Yatiniele, wachisanu Elamu, wachisanu ndi chimodzi Yehohanani, wachisanu ndi chiwiri Eliehoenai. Ndipo Obededomu anali nao ana, woyamba Semaya, wachiwiri Yehozabadi, wachitatu Yowa, wachinai Sakara, wachisanu Netanele, wachisanu ndi chimodzi Amiyele, wachisanu ndi chiwiri Isakara, wachisanu ndi chitatu Peuletai; pakuti Mulungu adamdalitsa. Kwa Semaya mwana wake yemwe kunabadwa ana, akulamulira nyumba ya atate wao; pakuti anali ngwazi zamphamvu. Ana a Semaya: Otini, ndi Refaele, ndi Obedi, Elizabadi, amene abale ao ndiwo odziwa mphamvu, Elihu, ndi Semakiya. Onsewa ndiwo a ana a Obededomu; iwo ndi ana ao, ndi abale ao, anthu odziwa mphamvu yakutumikira, makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri a Obededomu. Ndi Meselemiya anali ndi ana, ndi abale odziwa mphamvu khumi mphambu asanu ndi atatu. Hosa yemwe wa ana a Merari anali ndi ana, wamkulu ndi Simiri; pakuti ngakhale sanali wobadwa woyamba, atate wake anamuyesa wamkulu; wachiwiri Hilikiya, wachitatu Tebaliya, wachinai Zekariya; ana ndi abale onse a Hosa ndiwo khumi ndi atatu. Mwa iwowa munali magawidwe a odikira, mwa akulu a amuna akuchita udikiro wao, monga abale ao, kutumikira m'nyumba ya Yehova. Ndipo anachita maere ang'ono ndi akulu, monga mwa nyumba za makolo ao, kuchitira zipata zonse. Ndi maere a kum'mawa anagwera Selemiya. Ndipo anachitira maere Zekariya mwana wake, phungu wanzeru, ndi maere anamgwera kumpoto; Obededomu kumwera, ndi ana ake nyumba ya akatundu. Supimu ndi Hosa kumadzulo, ku chipata cha Saleketi, ku mseu wokwerapo, udikiro pandunji pa udikiro. Kum'mawa kunali Alevi asanu ndi mmodzi, kumpoto anai tsiku ndi tsiku, kumwera anai tsiku ndi tsiku, ndi a nyumba ya akatundu awiri ndi awiri. Ku Parabara kumadzulo anai kumseu, ndi awiri ku Parabara. Awa ndi magawidwe a odikira; a ana a Akora, ndi a ana a Merari. Ndipo wa Alevi, Ahiya anayang'anira chuma cha nyumba ya Mulungu, ndi chuma cha zopatulika. Ana a Ladani: ana a Ladani a Ageresoni, akulu a nyumba za makolo a Ladani Mgeresoni, Yehiyeli. Ana a Yehiyeli: Zetamu ndi Yowele mbale wake, oyang'anira chuma cha nyumba ya Yehova. Aamuramu, Aizihara, Ahebroni, Auziyele; ndi Sebuele mwana wa Geresomo, mwana wa Mose, ndiye mkulu woyang'anira zuma. Ndi abale ake a Eliyezere: Rehabiya mwana wake, ndi Yesaya mwana wake ndi Yoramu mwana wake, ndi Zikiri mwana wake, ndi Selomoti mwana wake. Selomoti amene ndi abale ake anayang'anira chuma chonse cha zinthu zopatulika, zimene Davide mfumu ndi akulu a nyumba za akulu, akulu a zikwi ndi mazana, adazipatula. Kutenga pa zofunkha kunkhondo, anapatulako kukonzera nyumba ya Yehova. Ndipo zonse adazipatula Samuele mlauli, ndi Saulo mwana wa Kisi, ndi Abinere mwana wa Nere, ndi Yowabu mwana wa Zeruya; aliyense anapatula kanthu kalikonse, anazisunga Selomoti ndi abale ake. A Aizihara: Kenaniya ndi ana ake anachita ntchito ya pabwalo ya Israele, akapitao ndi oweruza milandu. A Ahebroni: Hasabiya ndi abale ake odziwa mphamvu chikwi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri anayang'anira Israele tsidya lino la Yordani kumadzulo, kuyang'anira ntchito yonse ya Yehova, ndi kutumikira mfumu. Yeriya ndiye mkulu wa Ahebroni, wa Ahebroni monga mwa mibadwo ya nyumba za makolo. Chaka cha makumi anai cha ufumu wa Davide anafunafuna, napeza mwa iwowa ngwazi zamphamvu ku Yazere wa ku Giliyadi. Ndi abale ake ngwazi ndiwo zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri, akulu a nyumba za makolo, amene mfumu Davide anaika akhale oyang'anira a Arubeni, ndi Agadi, ndi fuko la Manase logawika pakati, pa zinthu zonse za Mulungu ndi zinthu za mfumu. Ndipo ana a Israele monga mwa chiwerengo chao, kunena za akulu a nyumba za makolo ao, ndi akazembe a zikwi, ndi a mazana, ndi akapitao ao akutumikira mfumu mu ntchito iliyonse ya magawidwe, akulowa ndi kutuluka mwezi ndi mwezi, miyezi yonse ya chaka, chigawo chilichonse ncha amuna zikwi makumi awiri mphambu zinai. Woyang'anira chigawo choyamba cha mwezi, woyamba ndiye Yasobeamu mwana wa Zabidiele; m'chigawo mwake munali zikwi makumi awiri mphambu zinai. Ndiye wa ana a Perezi, mkulu wa akazembe onse a khamu mwezi woyamba. Woyang'anira chigawo cha mwezi wachiwiri ndiye Dodai Mwahohi ndi chigawo chake; ndi Mikiloti mtsogoleri, ndi m'chigawo chake munali zikwi makumi awiri mphambu zinai. Kazembe wachitatu wa khamu wa mwezi wachitatu ndiye Benaya mwana wa Yehoyada wansembe wamkulu; ndi m'chigawo mwake munalinso zikwi makumi awiri mphambu zinai. Benaya ameneyo ndiye wamphamvu uja wa makumi atatu aja, woyang'anira chigawo chake ndi Amizabadi mwana wake. Wachinai wa mwezi wachinai ndiye Asahele mbale wa Yowabu, ndi pambuyo pake Zebadiya mwana wake; ndi m'chigawo mwake munali zikwi makumi awiri mphambu zinai. Kazembe wachisanu wa mwezi wachisanu ndiye Samuti Mwizara; ndi m'chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai. Wachisanu ndi chimodzi wa mwezi wachisanu ndi chimodzi ndiye Ira mwana wa Ikesi Mtekowa; ndi m'chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai. Wachisanu ndi chiwiri wa mwezi wachisanu ndi chiwiri ndiye Helezi Mpeloni wa ana a Efuremu; ndi m'chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai. Wachisanu ndi chitatu wa mwezi wachisanu ndi chitatu ndiye Sibekai Muhusa wa Azera; ndi m'chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai. Wachisanu ndi chinai wa mwezi wachisanu ndi chinai ndiye Abiyezere Mwanatoti wa Abenjamini; ndi m'chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai. Wakhumi wa mwezi wakhumi ndiye Maharai Mnetofa wa Azera; ndi m'chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai. Wakhumi ndi chimodzi wa mwezi wakhumi ndi chimodzi ndiye Benaya Mpiratoni wa ana a Efuremu; ndi m'chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai. Wakhumi ndi chiwiri wa mwezi wakhumi ndi chiwiri ndiye Helidai Mnetofa wa Otiniyele; ndi m'chigawo mwake zikwi makumi awiri mphambu zinai. Koma oyang'anira mafuko a Israele ndi awa: wa Arubeni mtsogoleri wao ndiye Eliyezere mwana wa Zikiri; wa Asimeoni, Sefatiya mwana wa Maaka; wa Alevi, Hasabiya mwana wa Kemuwele; wa Aroni, Zadoki; wa Yuda, Elihu mbale wina wa Davide; wa Isakara, Omuri mwana wa Mikaele; wa Zebuloni, Isimaya mwana wa Obadiya; wa Nafutali, Yerimoti mwana wa Aziriele; wa ana a Efuremu, Hoseya mwana wa Azaziya; wa fuko la Manase logawika pakati, Yowele mwana wa Pedaya; wa fuko la Manase logawika pakati m'Giliyadi, Ido mwana wa Zekariya; wa Benjamini, Yaasiyele mwana wa Abinere; wa Dani, Azarele mwana wa Yerohamu. Awa ndi akazembe a mafuko a Israele. Koma Davide sanawerenge iwo a zaka makumi awiri ndi ochepapo, pakuti Yehova adati kuti adzachulukitsa Israele ngati nyenyezi za kuthambo. Yowabu mwana wa Zeruya anayamba kuwerenga, koma sanatsirize; ndi mkwiyo unagwera Israele chifukwa cha ichi, ndipo chiwerengo chao sichinalembedwa m'buku la mbiri ya mfumu Davide. Ndipo woyang'anira chuma cha mfumu ndiye Azimaveti mwana wa Adiyele, ndi woyang'anira wa chuma cha m'minda, m'mizinda ndi m'milaga, ndi nyumba za nsanja, ndiye Yonatani mwana wa Uziya; ndi woyang'anira iwo akugwira ntchito ya m'munda yakulima nthaka ndiye Eziri mwana wa Kelubu; ndi woyang'anira minda yamphesa ndiye Simei Mramati; ndi woyang'anira zipatso za minda yamphesa zisungike mosungiramo vinyo ndiye Zabidi Msifamu; ndi woyang'anira mitengo ya azitona, ndi yamikuyu yokhala kuzidikha kunsi, ndiye Baala-Hanani Mgederi; ndi woyang'anira zosungiramo mafuta ndiye Yowasi; ndi woyang'anira ng'ombe zakudya m'Saroni ndiye Sitirai Msaroni; ndi woyang'anira ng'ombe za m'zigwa ndiye Safati mwana wa Adilai; ndi woyang'anira ngamira ndiye Obili Mwismaele; ndi woyang'anira abulu ndiye Yedeiya Mmeronoti; ndi woyang'anira zoweta zazing'ono ndiye Yazizi Mhagiri. Onsewa ndiwo akulu a zolemera zake za mfumu Davide. Ndipo Yonatani atate wake wina wa Davide anali phungu, munthu wanzeru ndi mlembi; ndi Yehiyele mwana wa Hakimoni anakhala ndi ana a mfumu; ndi Ahitofele anali phungu wa mfumu, ndi Husai Mwariki anali bwenzi la mfumu; ndi wotsatana ndi Ahitofele, Yehoyada mwana wa Benaya, ndi Abiyatara; koma kazembe wa nkhondo ya mfumu ndiye Yowabu. Pamenepo Davide anasonkhanitsa ku Yerusalemu akalonga a Israele, akalonga a mafuko, ndi akulu a zigawo zakutumikira mfumu, ndi akulu a zikwi, ndi akulu a mazana, ndi akulu a zolemera zonse, ndi zoweta zonse za mfumu, ndi ana ake; pamodzi ndi akapitao ndi anthu amphamvu, ndiwo ngwazi zamphamvu onsewo. Ndipo mfumu Davide anaima chilili, nati, Mundimvere ine, abale anga ndi anthu anga, ine kumtima kwanga ndinafuna kulimangira likasa la chipangano la Yehova, ndi popondapo mapazi a Mulungu wathu nyumba yopumulira, ndipo ndidakonzeratu za nyumbayi. Koma Mulungu anati kwa ine, Sudzamangira dzina langa nyumba, popeza ndiwe munthu wa nkhondo wokhetsa mwazi. Komatu Yehova Mulungu wa Israele anasankha ine m'nyumba yonse ya atate wanga, ndikhale mfumu ya Israele kosatha; pakuti anasankhiratu Yuda akhale mtsogoleri, ndi m'nyumba ya Yuda nyumba ya atate wanga, ndi mwa ana a atate wanga ndinamkomera ndine, andilonge ufumu wa Israele yense; ndi mwa ana anga onse (pakuti Yehova wandipatsa ana amuna ambiri), anasankha Solomoni mwana wanga akhale pa mpando wachifumu wa ufumu wa Yehova kuweruza Israele. Ndipo anati kwa ine, Solomoni mwana wako ndiye adzandimangira nyumba yanga ndi mabwalo anga; pakuti ndamsankha akhale mwana wanga, ndipo Ine ndidzakhala atate wake. Ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake kosatha, akalimbika kuchita malamulo anga ndi maweruzo anga monga lero lino. Ndipo tsopano, pamaso pa Aisraele onse, khamu la Yehova, ndi m'makutu a Mulungu wathu, sungani, nimufunefune malamulo onse a Yehova Mulungu wanu, kuti mukhale nalo lanulanu dziko lokoma ili, ndi kulisiyira ana anu pambuyo panu cholowa chao kosalekeza. Ndipo iwe Solomoni mwana wanga, umdziwe Mulungu wa atate wako, umtumikire ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu; pakuti Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo; ukamfunafuna Iye udzampeza, koma ukamsiya Iye adzakusiya kosatha. Chenjera tsono, pakuti Yehova anakusankha iwe umange nyumba ya malo opatulika; limbika, nuchite. Pamenepo Davide anapatsa Solomoni mwana wake chifaniziro cha chipinda cholowera cha Kachisi, ndi cha nyumba zake, ndi cha zosungiramo chuma zake, ndi cha zipinda zosanjikizana zake, ndi cha zipinda zake za m'katimo, ndi cha Kachisi wotetezerepo; ndi chifaniziro cha zonse anali nazo mwa mzimu, cha mabwalo a nyumba ya Yehova, ndi cha zipinda zonse pozungulirapo, cha zosungiramo chuma cha nyumba ya Mulungu, ndi cha zosungiramo chuma za zinthu zopatulika; ndi cha magawidwe a ansembe ndi Alevi, ndi cha ntchito zonse za utumiki wa nyumba ya Yehova, ndi cha zipangizo za utumiki wa nyumba ya Yehova; cha golide woyesedwa kulemera kwake wa zipangizo zagolide, wa zipangizo zonse za ntchito ya mtundu uliwonse; cha siliva wa zipangizo zasiliva woyesedwa kulemera kwake, wa zipangizo za ntchito ya mitundumitundu; mwa kulemera kwakenso cha zoikapo nyali zagolide, ndi nyali zake zagolide, mwa kulemera kwake cha choikapo nyali chilichonse, ndi nyali zake; ndi cha zoikapo nyali zasiliva, siliva woyesedwa kulemera kwake wa choikapo nyali chilichonse, ndi nyali zake, monga mwa ntchito ya choikapo nyali chilichonse; ndi golide woyesedwa kulemera kwake wa magome a mkate woonekera, wa gome lililonse; ndi siliva wa magome asiliva, ndi mitengo, ndi mbale zowazira, ndi zikho za golide woona, ndi cha mitsuko yake yagolide, woyesedwa kulemera kwake mtsuko uliwonse; ndi cha mitsuko yasiliva woyesedwa kulemera kwake mtsuko uliwonse; ndi cha guwa la nsembe lofukizapo la golide woyengetsa woyesedwa kulemera kwake, ndi chifaniziro cha galeta wa akerubi agolide akufunyulula mapiko ao ndi kuphimba likasa la chipangano la Yehova. Chonsechi, anati Davide, anandidziwitsa ndi kuchilemba kuchokera kwa dzanja la Yehova; ndizo ntchito zonse za chifaniziro ichi. Ndipo Davide anati kwa Solomoni mwana wake, Limbika, nulimbe mtima, nuchichite; usaopa, kapena kutenga nkhawa; pakuti Yehova Mulungu, ndiye Mulungu wanga, ali nawe; sadzakusowa kapena kukutaya mpaka zitatha ntchito zonse za utumiki wa nyumba ya Yehova. Ndipo taona, pali zigawo za ansembe ndi Alevi, za utumiki wonse wa nyumba ya Mulungu; ndipo pamodzi nawe mu ntchito iliyonse pali onse ofuna eni ake aluso, achite za utumiki uliwonse; akulu omwe ndi anthu onse adzachita monga umo udzanenamo. Mfumu Davide ananenanso kwa khamu lonse, Mulungu wasankha mwana wanga Solomoni yekha, ndiye mnyamata ndi wosakhwima; ndipo ntchitoyi ndi yaikulu, pakuti chinyumbachi sichili cha munthu, koma cha Yehova Mulungu. Ndi mphamvu yanga yonse tsono ndakonzeratu nyumba ya Mulungu wanga, golide wa zija zagolide ndi siliva wa zija zasiliva, ndi mkuwa wa zija zamkuwa, chitsulo cha zija zachitsulo, ndi mtengo wa zija zamtengo, miyala yaberulo, ndi miyala yoikika, miyala yokometsera, ndi ya mawangamawanga, ndi miyala ya mtengo wake ya mitundumitundu ndi miyala yansangalabwe yochuluka. Ndiponso popeza ndikondwera nayo nyumba ya Mulungu wanga, chuma changachanga cha golide ndi siliva ndili nacho ndichipereka kunyumba ya Mulungu wanga, moonjezera ndi zonse ndazikonzeratu nyumba yopatulikayo; ndicho matalente zikwi zitatu za golide, golide wa Ofiri; ndi matalente zikwi zisanu ndi ziwiri a siliva woyengetsa, kumamatiza nazo makoma a nyumbazi; golide wa zija zagolide, ndi siliva wa zija zasiliva, ndi za ntchito zilizonse akuzipanga manja a amisiri. Ndani uyo afuna mwini kudzipatulira kwa Yehova lero lino? Pamenepo akulu a nyumba za makolo, ndi akulu a mafuko a Israele, ndi akulu a zikwi ndi a mazana pamodzi ndi iwo oyang'anira ntchito ya mfumu, anapereka mwaufulu, napereka ku utumiki wa nyumba ya Mulungu golide matalente zikwi zisanu, ndi madariki zikwi khumi; ndi siliva matalente zikwi khumi, ndi mkuwa matalente zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu, ndi chitsulo matalente zikwi zana limodzi. Ndipo amene anali nayo miyala ya mtengo wake anaipereka ku chuma cha nyumba ya Yehova, mwa dzanja la Yehiyele Mgeresoni. Ndipo anthu anakondwera popeza anapereka mwaufulu; pakuti ndi mtima wangwiro anapereka mwaufulu kwa Yehova; mfumu Davide yemwe anakondwera ndi chimwemwe chachikulu. Motero Davide analemekeza Yehova pamaso pa khamu lonse, nati Davide, Wolemekezedwa Inu, Yehova Mulungu wa Israele, Atate wathu ku nthawi zomka muyaya. Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi chipambano, ndi chifumu ndi zanu, Yehova; pakuti zonse zam'mwamba ndi pa dziko lapansi ndi zanu; ufumu ndi wanu, Yehova; ndipo mwakwezeka mutu wa pa zonse. Zolemera ndi ulemu zifuma kwanu, ndipo muchita ufumu pa zonse, ndi m'dzanja mwanu muli mphamvu yaikulu; kukuza ndi kupatsa onse mphamvu kuli m'dzanja lanu. Motero tsono, Mulungu wathu, tikuyamikani ndi kulemekeza dzina lanu lokoma. Koma ndine yani, ndi anthu anga ndiwo ayani, kuti tidzakhoza kupereka mwaufulu motere? Popeza zonsezi zifuma kwanu; takupatsani zofuma ku dzanja lanu. Pakuti ife ndife alendo pamaso panu, ndi ogonera, monga makolo athu onse; masiku athu a padziko akunga mthunzi, ndipo palibe kukhalitsa. Yehova Mulungu wathu, zounjikika izi zonse tazikonzeratu kukumangirani Inu nyumba ya dzina lanu loyera zifuma ku dzanja lanu, zonsezi ndi zanu. Ndidziwanso, Mulungu wanga, kuti muyesa mtima, nimukondwera nako kuongoka. Koma ine, ndi mtima wanga woongoka ndapereka zonsezi mwaufulu; ndipo tsopano ndaona mokondwera anthu anu okhala pompano, napereka kwa Inu mwaufulu. Yehova Mulungu wa Abrahamu, wa Isaki, ndi wa Israele makolo athu, musungitse ichi kosatha m'chilingaliro cha maganizo a mtima wa anthu anu, nimulunjikitse mitima yao kwanu, nimupatse Solomoni mwana wanga mtima wangwiro kusunga malamulo anu, mboni zanu, ndi malemba anu, ndi kuchita izi zonse, ndi kumanga chinyumbachi chimene ndakonzeratu mirimo yake. Ndipo Davide anati kwa khamu lonse, Mulemekeze tsono Yehova Mulungu wanu. Ndi khamu lonse linalemekeza Yehova Mulungu wa makolo ao, nawerama, nalambira Yehova, ndi mfumu. Ndipo anamphera Yehova nsembe, napereka nsembe zopsereza kwa Yehova m'mawa mwake mwa tsiku lija, ndizo ng'ombe chikwi chimodzi, nkhosa zamphongo chikwi chimodzi, ndi anaankhosa chikwi chimodzi, pamodzi ndi nsembe zao zothira, ndi nsembe zochuluka za Aisraele onse: nadya namwa pamaso pa Mulungu tsiku lomwelo ndi chimwemwe chachikulu. Ndipo analonga ufumu Solomoni mwana wa Davide kachiwiri, namdzozera Yehova akhale kalonga, ndi Zadoki akhale wansembe. Momwemo Solomoni anakhala pa mpando wachifumu wa Yehova, ndiye mfumu m'malo mwa Davide atate wake, nalemerera, namvera iye Aisraele onse. Ndi akulu onse, ndi amuna amphamvu onse, ndi ana amuna onse omwe a mfumu Davide, anagonjeratu kwa Solomoni mfumu. Ndipo Yehova anakuza Solomoni kwakukulu pamaso pa Aisraele onse, nampatsa ulemerero wachifumu, wakuti, asanakhale iyeyu, panalibe mfumu ya Israele inali nao wotero. Momwemo Davide mwana wa Yese adakhala mfumu ya Aisraele onse. Ndipo nthawi yoti anakhala mfumu ya Israele ndiyo zaka makumi anai; zaka zisanu ndi ziwiri anakhala mfumu m'Hebroni, ndi zaka makumi atatu anakhala mfumu m'Yerusalemu. Nafa atakalamba bwino, wochuluka masiku, zolemera, ndi ulemerero; ndi Solomoni mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake. Zochita mfumu Davide tsono, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zalembedwa m'buku la mau a Samuele mlauli, ndi m'buku la mau a Natani mneneri, ndi m'buku la mau a Gadi mlauli; pamodzi ndi za ufumu wake wonse, ndi mphamvu yake, ndi za nthawizo zidampitira iye, ndi Israele, ndi maufumu onse a maiko. Ndipo Solomoni mwana wa Davide analimbikitsidwa m'ufumu wake, ndipo Yehova Mulungu wake anali naye, namkuza kwakukulu. Ndipo Solomoni analankhula ndi Aisraele onse, ndi akulu a zikwi ndi a mazana, ndi kwa oweruza, ndi kwa kalonga aliyense wa Israele, akulu a nyumba za makolo. Ndipo Solomoni ndi khamu lonse pamodzi naye anamuka ku msanje wa ku Gibiyoni; pakuti kumeneko kunali chihema chokomanako cha Mulungu adachimanga Mose mtumiki wa Yehova m'chipululu. Koma likasa la Mulungu Davide adakwera nalo kuchokera ku Kiriyati-Yearimu kunka kumene Davide adalikonzeratu malo; pakuti adaliutsiratu hema ku Yerusalemu. Guwa la nsembe lomwe lamkuwa, adalipanga Bezalele mwana wa Uri mwana wa Huri linali komweko, ku khomo la Kachisi wa Yehova; ndipo Solomoni ndi khamulo anafunako. Nakwerako Solomoni ku guwa la nsembe pamaso pa Yehova linali ku chihema chokomanako, napereka pamenepo nsembe zopsereza chikwi chimodzi. Usiku womwewo Mulungu anaonekera kwa Solomoni, nati kwa iye, Pempha chomwe ndikupatse. Nati Solomoni kwa Mulungu, Mwachitira Davide atate wanga zokoma zambiri, ndipo mwandiika mfumu m'malo mwake. Tsopano, Yehova Mulungu, likhazikike lonjezano lanu la kwa Davide atate wanga; pakuti mwandiika mfumu ya anthu akuchuluka ngati fumbi lapansi. Mundipatse tsono nzeru ndi chidziwitso, kuti ndituluke ndi kulowa pamaso pa anthu awa; pakuti angathe ndani kuweruza anthu anu awa ambiri? Ndipo Mulungu anati kwa Solomoni, Popeza chinali mumtima mwako ichi, osapempha chuma, akatundu, kapena ulemu, kapena moyo wa iwo akudana nawe, osapemphanso masiku ambiri; koma wadzipemphera nzeru ndi chidziwitso, kuti uweruze anthu anga amene ndakuika ukhale mfumu yao, nzeru ndi chidziwitso zipatsidwa kwa iwe, ndidzakupatsanso chuma, ndi akatundu, ndi ulemu, zotere zonga sanakhale nazo mafumu akale usanakhale iwe, ndi akudza pambuyo pako sadzakhala nazo zotero. Momwemo Solomoni anadza ku Yerusalemu kuchokera ku msanje uli ku Gibiyoni, ku khomo la chihema chokomanako; ndipo anachita ufumu pa Israele. Ndipo Solomoni anasonkhanitsa magaleta ndi apakavalo, nakhala nao magaleta chikwi chimodzi mphambu mazana anai, ndi apakavalo zikwi khumi ndi ziwiri; nawaika m'midzi ya magaleta ndi kwa mfumu ku Yerusalemu. Ndipo mfumu inatero kuti siliva ndi golide zikhale m'Yerusalemu ngati miyala, ndi kuti mikungudza ichuluke ngati mikuyu yokhala kuchidikha. Ndi akavalo amene Solomoni anali nao anafuma ku Ejipito; amalonda a mfumu anawalandira magulumagulu, gulu lililonse mtengo wake. Ndipo anatenga natuluka nalo galeta ku Ejipito mtengo wake masekeli a siliva mazana asanu ndi limodzi, ndi kavalo mtengo wake zana limodzi mphambu makumi asanu; momwemo anawatulutsira mafumu onse a Ahiti, ndi mafumu a Aramu, ndi dzanja lao. Ndipo Solomoni anati alimangire dzina la Yehova nyumba, ndiponso nyumba ya ufumu wake. Nawerenga Solomoni amuna zikwi khumi mphambu makumi asanu ndi limodzi osenza mirimo, ndi amuna zikwi makumi asanu ndi atatu otema mitengo m'mapiri, ndi zikwi zitatu mphambu mazana asanu ndi limodzi kuwayang'anira. Ndipo Solomoni anatumiza kwa Huramu mfumu ya Tiro, ndi kuti, Monga momwe munachitira Davide atate wanga, ndi kumtumizira mikungudza yommangira nyumba yokhalamo, mundichitire ine momwemo. Taonani, nditi ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba, kumpatulira iyo, ndi kufukiza pamaso pake zonunkhira za fungo lokoma, ndiyo ya mkate woonekera wachikhalire, ndi ya nsembe zopsereza, m'mawa ndi madzulo, pamasabata, ndi pokhala mwezi, ndi pa zikondwerero zoikika za Yehova Mulungu wathu. Ndiwo machitidwe osatha m'Israele. Ndipo nyumba nditi ndimangeyi ndi yaikulu; pakuti Mulungu wathu ndiye wamkulu woposa milungu yonse. Koma ali nayo mphamvu ndani yakummangira Iye nyumba, popeza thambo lam'mwambamwamba silimfikira? Ndine yani ine tsono, kuti ndimmangire nyumba, koma kumfukizira chofukiza ndiko? Ndipo tsono munditumizire munthu waluso lakuchita ndi golide, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, ndi thonje lofiirira, ndi lofiira, ndi lamadzi, wakudziwa kuzokota zozokota zilizonse, akhale ndi amuna aluso okhala ndi ine m'Yuda ndi m'Yerusalemu, amene Davide atate wanga anawakonzeratu. Munditumizirenso mitengo yamikungudza, ndi yamlombwa, ndi yambawa, ya ku Lebanoni; pakuti ndidziwa kuti anyamata anu adziwa kutema mitengo m'Lebanoni; ndipo taonani, anyamata anga adzakhala ndi anyamata anu, ndiko kundikonzera mitengo yambirimbiri; pakuti nyumbayi nditi ndiimange idzakhala yaikulu ndi yodabwitsa. Ndipo taonani, ndidzawapatsa anyamata anu otema akulikha mitengo miyeso ya tirigu wopuntha zikwi makumi awiri, ndi miyeso ya barele zikwi makumi awiri, ndi mitsuko yaikulu ya vinyo zikwi makumi awiri, ndi mitsuko yaikulu ya mafuta zikwi makumi awiri. Ndipo Huramu mfumu ya Tiro anayankha ndi kulembera, natumiza kalatayo kwa Solomoni, ndi kuti, Powakonda anthu ake Yehova anakulongani mfumu yao. Huramu anatinso, Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israele, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nampatsa mfumu Davide mwana waluso, wodziwa nzeru ndi waluntha, ammangire Yehova nyumba, ndiponso nyumba ya ufumu wake. Ndipo tsono ndatumiza munthu waluso wokhala nalo luntha, Huramuabi, ndiye mwana wa munthu wamkazi wa ana akazi a Dani, ndipo atate wake ndiye munthu wa ku Tiro, wodziwa kuchita ndi golide, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, ndi mwala, ndi mitengo, ndi thonje lofiirira, ndi lamadzi, ndi bafuta la thonje losansitsa ndi lofiira, ndi kuzokota mazokotedwe ali onse, ndi kulingirira chopanga chilichonse; kuti ampatse pokhala pamodzi ndi aluso anu, ndi aluso a mbuye wanga Davide atate wanu. Ndipo tsono tirigu ndi barele, mafuta ndi vinyo, mbuye wanga wanenazi, azitumize kwa anyamata ake; ndipo ife tidzatema mitengo ku Lebanoni monga mwa kusowa kwanu konse; ndipo tidzabwera nayo kwa inu yoyandamitsa paphaka kufikira ku Yopa; ndipo inu mudzakwera nayo ku Yerusalemu. Ndipo Solomoni anawerenga alendo onse okhala m'dziko la Israele, monga mwa mawerengedwe aja atate wake Davide adawawerenga nao, nawapeza afikira zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu kudza zitatu ndi mazana asanu ndi limodzi. Ndipo anaika zikwi makumi asanu ndi awiri za iwowa asenze mirimo, ndi zikwi makumi asanu ndi atatu ateme m'mapiri, ndi akapitao zikwi zitatu mphambu mazana asanu ndi limodzi agwiritse anthu ntchito. Pamenepo Solomoni anayamba kumanga nyumba ya Yehova ku Yerusalemu, m'phiri la Moriya, kumene Mulungu anaonekera kwa Davide atate wake pamalo pamene Davide anakonzeratu pa dwale la Orinani Myebusi. Nayamba kumanga tsiku lachiwiri la mwezi wachiwiri, chaka chachinai cha ufumu wake. Ndipo maziko adawaika Solomoni akumangapo nyumba ya Mulungu ndi awa: utali wake, kuyesa mikono monga mwa muyeso wakale, ndiwo mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri. Ndi chipinda cholowera chinali kukhomo kwa nyumba, m'litali mwake monga mwa kupingasa kwa nyumba munali mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake zana limodzi mphambu makumi awiri; ndipo analikuta m'katimo ndi golide woona. M'nyumba yaikulu tsono anatchinga ndi mitengo yamlombwa, imene anaikuta ndi golide wabwino, nalembapo ngati migwalangwa ndi maunyolo. Ndipo anakuta nyumba ndi miyala ya mtengo wake; ndi golide wake ndiye golide wa Paravaimu. Anamamatizanso Kachisi, mitanda, ziundo, ndi makoma ake, ndi zitseko zake, ndi golide; nalemba akerubi pamakoma. Ndipo anamanga malo opatulika kwambiri, m'litali mwake monga mwa kupingasa kwa nyumba mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri; naikuta ndi golide wabwino wakufikira matalente mazana asanu ndi limodzi. Ndi kulemera kwake kwa misomali ndiko masekeli makumi asanu a golide. Ndipo anazikuta ndi golide zipinda zosanjikizana. Ndipo m'malo opatulika kwambiri anapanga akerubi awiri, anachita osema, nawakuta ndi golide. Ndi mapiko a akerubi m'litali mwake ndimo mikono makumi awiri; phiko la kerubi mmodzi mikono isanu, lojima khoma la nyumba; ndi phiko linzake mikono isanu, lokhudzana nalo phiko la kerubi wina. Ndi phiko la kerubi wina mikono isanu lojima khoma la nyumba, ndi phiko linzake mikono isanu lolumikizana ndi phiko la kerubi wina. Mapiko a akerubi awa anafunyululika mikono makumi awiri; ndipo anaima ndi mapazi ao, ndi nkhope zao zinaloza kukhomo. Ndipo anaomba nsalu yotchinga ya thonje lamadzi, ndi lofiira, ndi lofiirira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, naomberamo akerubi. Ndipo anapanga ku khomo la nyumba nsanamira ziwiri za mikono makumi atatu mphambu ziwiri; ndi mutu unakhala pamwamba pa iliyonse ndiwo mikono isanu. Napanga maunyolo a m'chipinda chamkati, nawamanga pa mitu ya nsanamirazi, napanga makangaza zana limodzi, nawamanga pamaunyolo. Ndipo anaimiritsa nsanamirazo pakhomo pa Kachisi; imodzi ku dzanja lamanja, ndi inzake ku dzanja lamanzere; nalitcha dzina la iyi ya ku dzanja lamanja Yakini, ndi dzina la iyi ya ku dzanja lamanzere Bowazi. Anapanganso guwa la nsembe lamkuwa, m'litali mwake mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake mikono khumi. Anayenganso thawale losungunula la mikono khumi kukamwa, lozunguniza, ndi msinkhu wake mikono isanu; ndi chingwe cha mikono makumi atatu chinalizunguniza. Ndi pansi pake panali mafaniziro a ng'ombe zakulizinga, khumi ku mkono umodzi, zakuzinga thawalelo pozungulira pake. Ng'ombe zinali m'mizere iwiri, zinayengeka poyengedwa thawalelo. Linasanjikika pa ng'ombe khumi ndi ziwiri, zitatu zinapenya kumpoto, ndi zitatu zinapenya kumadzulo, ndi zitatu zinapenya kumwera, ndi zitatu zinapenya kum'mawa; ndi thawale linasanjikika pamwamba pao, ndi nkholo zao zinayang'anana. Ndi kuchindikira kwake kunanga chikhato, ndi mlomo wake unasadamuka ngati mlomo wa chomwera, ngati luwa la kakombo; analowamo madzi a mitsuko yaikulu zikwi zitatu. Anapanganso mbiya zaphwamphwa khumi, naika zisanu ku dzanja lamanja, ndi zisanu ku dzanja lamanzere, kutsukiramo; za nsembe yopsereza anazitsuka m'menemo; koma thawale ndi la ansembe kusambiramo. Ndipo anapanga zoikapo nyali khumi zagolide, monga mwa ziweruzo chake; naziika m'Kachisi, zisanu ku dzanja lamanja, ndi zisanu ku dzanja lamanzere. Anapanganso magome khumi, nawaika m'Kachisi, asanu ku dzanja lamanja, ndi asanu ku dzanja lamanzere. Napanga mbale zowazira zana limodzi zagolide. Anamanganso bwalo la ansembe, ndi bwalo lalikulu, ndi zitseko za kubwalo, nakuta zitseko zake ndi mkuwa. Ndipo anaika thawalelo ku dzanja lamanja la nyumba kum'mawa chakumwera. Ndipo Huramu anapanga miphika, ndi zoolera zake, ndi mbale zowazira zake. Natsiriza Huramu ntchito adaichitira mfumu Solomoni m'nyumba ya Mulungu: nsanamira ziwiri, ndi zikhozo, ndi mitu iwiri inali pamwamba pa nsanamirazo, ndi maukonde awiri akukuta zikho ziwiri za mitu ili pamwamba pa nsanamirazo, ndi makangaza mazana anai a maukonde awiriwa; mizere iwiri ya makangaza ya ukonde uliwonse, akukuta zikho ziwiri za mitu, inali pa nsanamirazo. Anapanganso maphaka, napanga mbiya zaphwamphwa khumi pamwamba pa maphaka; thawale limodzi ndi ng'ombe khumi ndi ziwiri pansi pake. Miphika yomwe, ndi zoolera, ndi mitungo, ndi zipangizo zake zonse, Huramuabi anazipangira mfumu Solomoni, kuzipangira nyumba ya Yehova, za mkuwa wonyezimira. Mfumuyi inaziyenga pa chidikha cha ku Yordani, m'dothi ladongo, pakati pa Sukoti ndi Zereda. Ndipo Solomoni anazipanga zipangizo izi zonse zochulukadi, pakuti kulemera kwake kwa mkuwa sikunayeseka. Solomoni anapanganso zipangizo zonse zinali m'nyumba ya Mulungu, guwa la nsembe lagolide lomwe, ndi magome oikapo mkate woonekera; ndi zoikapo nyali ndi nyali zake za golide woona, zakuunikira monga mwa chilangizo chake chakuno cha chipinda chamkati; ndi maluwa, ndi nyali, ndi mbano zagolide, ndiwo golide wangwiro; ndi zozimira nyali, ndi mbale zowazira, ndi zipande, ndi mbale za zofukiza za golide woona; ndi kunena za polowera m'nyumba, zitseko zake za m'katimo za malo opatulika kwambiri, ndi zitseko za nyumbayi, ndiyo Kachisi, zinali zagolide. Momwemo zidatha ntchito zonse Solomoni adazichitira nyumba ya Yehova. Ndipo Solomoni anabwera nazo zopatulika zija za atate wake Davide; naziika siliva, ndi golide, ndi zipangizo zonse m'chuma cha nyumba ya Mulungu. Pamenepo Solomoni anasonkhanitsira akuluakulu a Israele, ndi akulu onse a mafuko, ndi akalonga a nyumba za makolo a ana a Israele, ku Yerusalemu, kukatenga likasa la chipangano cha Yehova kumudzi wa Davide ndiwo Ziyoni. Ndipo amuna onse a Israele anasonkhana kwa mfumu kumadyerero anachitikawo, m'mwezi wachisanu ndi chiwiri. Nadza akuluakulu onse a Israele, nanyamula likasalo Alevi. Ndipo anakwera nalo likasa, ndi chihema chokomanako, ndi zipangizo zonse zopatulika zinali m'chihemamo; izizo ansembe Alevi anakwera nazo. Ndi mfumu Solomoni ndi khamu lonse la Israele losonkhana kwa iye anali kulikasa, naphera nsembe, nkhosa ndi ng'ombe zosawerengeka kuchuluka kwake. Ndipo ansembe analowa nalo likasa la chipangano la Yehova kumalo kwake m'chipinda chamkati mwa Kachisi, m'malo opatulika kwambiri, pansi pa mapiko a akerubi. Pakuti akerubi anafunyulula mapiko ao pa malo a likasa, ndi akerubi anaphimba likasa ndi mphiko zake pamwamba pake. Ndipo zinatalikitsa mphikozo, kuti nsonga za mphiko zidaoneka kulikasa chakuno cha chipinda chamkati, koma sizinaoneka kubwalo; ndipo zili komweko mpaka lero lino. Munalibe kanthu kena m'likasa, koma magome awiri Mose anawaika m'mwemo ku Horebu, muja Yehova anachita chipangano ndi ana a Israele potuluka iwo m'Ejipito. Ndipo ansembe anatuluka m'malo opatulika, pakuti ansembe onse anali komwe adadzipatula, osasunga magawidwe ao; Alevi omwe akuimba, onsewo ndiwo Asafu, Hemani, Yedutuni, ndi ana ao, ndi abale ao ovala bafuta, ali nazo nsanje, ndi zisakasa, ndi azeze, anaima kum'mawa kwa guwa la nsembe, ndi pamodzi nao ansembe zana limodzi mphambu makumi awiri akuomba malipenga. Ndipo kunali, pakuchita limodzi amalipenga ndi oimba, kumveketsa mau amodzi akulemekeza ndi kuyamika Yehova, ndi pakukweza mau ao pamodzi ndi malipenga, ndi nsanje, ndi zoimbira zina, ndi kulemekeza Yehova, ndi kuti, Pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire; pamenepo mtambo unadzaza nyumbayi, ndiyo nyumba ya Yehova; ndipo ansembe sanakhoze kuimirira kutumikira chifukwa cha mtambowo; pakuti ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Mulungu. Pamenepo Solomoni anati, Yehova anati kuti adzakhala mu mdima wandiweyani. Koma ndakumangirani nyumba yokhalamo, malo okhazikika okhalamo Inu nthawi yosatha. Ndipo mfumu inapotolokera nkhope yake, nidalitsa khamu lonse la Israele; ndi khamu lonse la Israele linaimirira. Nati iye, Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israele, wakunena m'kamwa mwake ndi Davide atate wanga, nakwaniritsa ndi manja ake, ndi kuti, Kuyambira tsiku lakutulutsa Ine anthu anga m'dziko la Ejipito, sindinasankha mudzi uliwonse m'mafuko onse a Israele, kumangamo nyumba yokhalamo dzina langa, kapena kusankha munthu aliyense akhale kalonga wa anthu anga Israele; Koma ndinasankha Yerusalemu, kuti dzina langa likhale komweko; ndinasankhanso Davide akhale mfumu ya anthu anga Israele. Ndipo Davide atate wanga anafuna mumtima mwake kumangira dzina la Yehova Mulungu wa Israele nyumba. Koma Yehova anati kwa Davide atate wanga, Popeza unafuna mumtima mwako kulimangira dzina langa nyumba, unachita bwino kuti unatero mumtima mwako; koma sudzandimangira nyumba ndiwe, koma mwana wako wakudzatuluka m'chuuno mwako, iyeyo adzalimangira dzina langa nyumbayi. Ndipo Yehova wakhazikitsa mau ake adanenawo, pakuti ndinauka ine m'malo mwa Davide atate wanga, ndipo ndikhala pa mpando wachifumu wa Israele monga analonjeza Yehova, ndipo ndamangira dzina la Yehova Mulungu wa Israele nyumbayi. Ndipo ndalongamo likasa, muli chipangano cha Yehova, anachichita ndi ana a Israele. Ndipo Solomoni anaima ku guwa la nsembe la Yehova pamaso pa khamu lonse la Israele, natambasula manja ake. Ndipo Solomoni adapanga chiunda chamkuwa, m'litali mwake mikono isanu, ndi msinkhu wake mikono itatu, nachiika pakati pa bwalo; ndipo anaima pamenepo nagwada pa maondo ake pamaso pa khamu lonse la Israele, natambasulira manja ake kumwamba; nati, Yehova Mulungu wa Israele, palibe Mulungu ngati Inu, m'mwamba, kapena pa dziko lapansi, wakusungira chipangano ndi chifundo akapolo anu akuyenda pamaso panu ndi mtima wao wonse; inu amene mwasungira mtumiki wanu Davide atate wanga chija mudamlonjezachi: inde munanena ndi pakamwa panu, ndipo mwachita ndi dzanja lanu, monga momwe muli lero lino. Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israele, msungireni mtumiki wanu Davide chija mudamlonjezacho, ndi kuti, Sadzakusowa munthu pamaso panga wakukhala pa mpando wachifumu wa Israele; pokhapo ngati ana ako asamalira njira yao, kuti ayende m'chilamulo changa, monga umo unayendera iwe pamaso panga. Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israele, achitike mau anu amene munanena kwa Davide mtumiki wanu. Koma kodi nzoona kuti Mulungu akhala ndi anthu pa dziko lapansi? Taonani, thambo, inde m'mwambamwamba, sizifikira inu, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimanga? Chinkana chitero, labadirani pemphero la kapolo wanu, ndi pembedzero lake, Yehova Mulungu wanga, kumvera kufuula ndi kupempha kwake, kumene kapolo wanu apempha pamaso panu; kuti maso anu atsegukire nyumba iyi usana ndi usiku, malo amene munanenerako kuti mudzaikako dzina lanu, kuti mumvere pemphero limene kapolo wanu adzapempha kuloza konkuno. Ndipo mverani mapembedzero a kapolo wanu ndi a anthu anu Israele, popemphera iwo kuloza konkuno; ndipo mumvere Inu m'Mwamba mokhala Inumo, ndipo pakumva Inu, mukhululukire. Munthu akachimwira mnansi wake, ndipo akamuikira lumbiro lakumlumbiritsa, ndipo akadzalumbira ku guwa lanu la nsembe, m'nyumba yino; pamenepo mumvere m'Mwamba, nimuchite ndi kuweruzira akapolo anu, kumtsutsa woipayo, ndi kumbwezera tchimo lake, ndi kulungamitsa wolungamayo, kumbwezera monga mwa chilungamo chake. Ndipo anthu anu Israele akawakantha mdani chifukwa cha kukuchimwirani, nakabwerera iwowa ndi kuvomereza dzina lanu, ndi kupemphera, ndi kupembedzera pamaso panu m'nyumba yino; pamenepo mumvere Inu m'Mwamba, nimukhululukire tchimo la anthu anu Israele, ndi kuwabwezera ku dziko limene munapatsa makolo ao. Mukatsekeka m'mwamba, mopanda mvula, chifukwa cha kukuchimwirani; akapemphera iwo kuloza kumalo kuno, ndi kuvomereza dzina lanu, ndi kutembenuka kwa zoipa zao, pamene muwasautsa; pamenepo mumvere Inu m'Mwamba, nimukhululukire tchimo la akapolo anu, ndi la anthu anu Israele, mutawalangiza njira yokoma ayenera kuyendamo, nimutumizire mvula dziko lanu limene munapatsa anthu anu likhale cholowa chao. Mukakhala njala m'dzikomo, mukakhala mliri, mukakhala chinsikwi, kapena chinoni, dzombe, kapena kapuche; akawamangira misasa adani ao, m'dziko la midzi yao; mukakhala mliri uliwonse, kapena nthenda iliyonse; pemphero ndi pembedzero lililonse likachitika ndi munthu aliyense, kapena ndi anthu anu onse Aisraele, akadziwa yense chinthenda chake, ndi chisoni chake, nakatambasulira manja ake kuloza kunyumba iyi: pamenepo mumvere m'Mwamba mokhala Inumo, nimukhululukire, ndi kubwezera aliyense monga mwa njira zake zonse, monga mudziwa mtima wake; pakuti Inu, Inu nokha, mudziwa mitima ya ana a anthu; kuti aope Inu kuyenda m'njira zanu masiku onse akukhala iwo m'dziko limene munapatsa makolo athu. Ndiponso kunena za mlendo wosakhala wa anthu anu Israele, akafumira ku dziko lakutali chifukwa cha dzina lanu lalikulu, ndi dzanja lanu lamphamvu, ndi mkono ndi kupemphera kuloza kunyumba iyi; pamenepo mumvere Inu m'Mwamba mokhala Inumo, nimumchitire mlendoyo monga mwa zonse akuitanirani; kuti mitundu yonse ya anthu a pa dziko lapansi adziwe dzina lanu, nakuopeni, monga amatero anthu anu Aisraele; ndi kuti adziwe kuti nyumba iyi ndamangayi itchedwa ndi dzina lanu. Akatulukira kunkhondo anthu anu kuyambana ndi adani ao, kutsata njira iliyonse muwatumiza; nakapemphera kwa Inu kuloza kumudzi uwu munausankha, ndi nyumba iyi ndaimangira dzina lanu; pamenepo mumvere m'Mwamba pemphero lao ndi pembedzero lao, ndi kulimbitsa mlandu wao. Akachimwira Inu (pakuti palibe munthu wosachimwa), nimukakwiya nao, ndi kuwapereka kwa adani, kuti awatenge andende kunka nao ku dziko lakutali, kapena lapafupi; koma akalingirira m'mtima mwao kudziko kumene anawatengera andende, nakatembenuka, nakapembedzera Inu m'dziko la undende wao, ndi kuti, Tachimwa, tachita mphulupulu, tachita choipa; akabwerera kwa Inu ndi mtima wao wonse, ndi moyo wao wonse, m'dziko la undende wao, kumene adawatengera andende; nakapemphera kuloza ku dziko lao limene munapatsa makolo ao, ndi mudzi mudausankha, ndi kunyumba ndamangira dzina lanuyi; pamenepo mumvere Inu m'Mwamba mokhala Inumo pemphero lao ndi pembedzero lao, ndi kulimbitsa mlandu wao; nimukhululukire anthu anu amene anakuchimwirani. Tsopano Mulungu wanga, maso anu akhale chipenyere, ndi makutu anu chimvere, pemphero lochitika pamalo pano. Ndipo tsopano nyamukani, Yehova Mulungu, kudza kopumulira kwanu, Inu ndi likasa la mphamvu yanu; ansembe anu, Yehova Mulungu, avale chipulumutso; ndi okondedwa anu akondwere nazo zabwino. Yehova Mulungu, musabweza nkhope ya wodzozedwa wanu, mukumbukire zachifundo za Davide mtumiki wanu. Atatha tsono Solomoni kupemphera, moto unatsika kumwamba, nunyeketsa nsembe yopsereza, ndi nsembe zophera; ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza nyumbayi. Ndipo ansembe sanakhoze kulowa m'nyumba ya Yehova, popeza ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehova. Ndi ana onse a Israele anapenyerera potsika motowo, ndi pokhala ulemerero wa Yehova panyumbayi; nawerama nkhope zao pansi poyalidwa miyala, nalambira, nayamika Yehova, nati, Pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire. Pamenepo mfumu ndi anthu onse anapereka nsembe pamaso pa Yehova. Ndipo mfumu Solomoni anapereka nsembe ya ng'ombe zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, ndi nkhosa zikwi makumi awiri. Momwemo mfumu ndi anthu onse anapereka nyumba ya Yehova. Naimirira ansembe m'udikiro wao; ndi Alevi omwe ndi zoimbira za Yehova, adazipanga Davide mfumu kuyamika nazo Yehova, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire, polemekeza Davide mwa utumiki wao; ndi ansembe anaomba malipenga pamaso pao, nakhala chilili Israele yense. Ndipo Solomoni anapatula pakati pake pa bwalo lili pakhomo pa nyumba ya Yehova; pakuti anapereka nsembe zopsereza, ndi mafuta a nsembe zoyamika pomwepo; popeza guwa la nsembe lamkuwa adalipanga Solomoni linachepa kulandira nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa, ndi mafuta. Nthawi yomweyo Solomoni anachita madyerero masiku asanu ndi awiri, ndi Aisraele onse pamodzi naye, khamu lalikulu ndithu, kuyambira polowera ku Hamati kufikira mtsinje wa ku Ejipito. Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu anachita msonkhano woletsa; popeza anachita zakupereka guwa la nsembe masiku asanu ndi awiri, ndi madyerero masiku asanu ndi awiri. Ndipo tsiku la makumi awiri ndi chitatu la mwezi wachisanu ndi chiwiri anawauza anthu apite ku mahema ao, akusekera ndi kukondwera m'mtima mwao chifukwa cha zokoma Yehova adawachitira Davide, ndi Solomoni, ndi Aisraele anthu ake. Momwemo Solomoni anatsiriza nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu; ndipo zilizonse zidalowa mumtima mwake mwa Solomoni kuzichita m'nyumba ya Yehova, ndi m'nyumba yakeyake, anachita mosalakwitsa. Ndipo Yehova anaonekera kwa Solomoni usiku, nanena naye, Ndamva pemphero lako, ndadzisankhira malo ano akhale nyumba ya nsembe. Ndikatseka kumwamba kuti pasakhale mvula, kapena ndikalamulira dzombe lithe za padziko, kapena ndikatumiza mliri mwa anthu anga; ndipo anthu anga otchedwa dzina langa akadzichepetsa, nakapemphera, nakafuna nkhope yanga, nakatembenuka kuleka njira zao zoipa; pamenepo ndidzamvera m'Mwamba, ndi kukhululukira choipa chao, ndi kuchiritsa dziko lao. Tsopano maso anga adzakhala otsegukira, ndi makutu anga otchera, pemphero la m'malo ano. Pakuti ndasankha ndi kuipatula nyumba iyi, kuti dzina langa likhaleko chikhalire; inde maso anga ndi mtima wanga zidzakhala komweko kosalekeza. Ndipo iwe ukadzayenda pamaso panga monga umo anayendera Davide atate wako, nukachita monga mwa zonse ndakulamulira iwe, nukasunga malemba anga ndi maweruzo anga; pamenepo ndidzakhazikitsa mpando wachifumu wa ufumu wako, monga ndinapangana ndi Davide atate wako, ndi kuti, Sadzakusowa munthu wokhala mfumu m'Israele. Koma mukabwerera inu, ndi kusiya malemba anga, ndi malamulo anga, amene ndaika pamaso panu, ndi kumuka ndi kutumikira milungu ina ndi kuilambira; pamenepo ndidzawazula m'dziko langa limene ndinawapatsa; ndi nyumba yino ndinaipatulira dzina langa ndidzaitaya, osaionanso, ndi kuiyesa mwambi ndi mnyozo mwa mitundu yonse ya anthu. Ndi munthu yense wakupita pa nyumba iyi yaitali adzadabwa nayo, nadzati, Yehova anatero ndi dziko lino ndi nyumba yino chifukwa ninji? Ndipo adzayankha, Popeza anasiya Yehova Mulungu wa makolo ao amene anawatulutsa m'dziko la Ejipito, nagwira milungu ina, nailambira ndi kuitumikira; chifukwa chake anawagwetsera choipa ichi chonse. Ndipo kunali, zitatha zaka makumi awiri m'mene Solomoni anamanga nyumba ya Yehova, ndi nyumba yakeyake, Solomoni anamanga midzi imene Huramu adampatsa, nakhalitsamo ana a Israele. Ndipo Solomoni anamuka ku Hamatizoba, naugonjetsa. Ndipo anamanga Tadimori m'chipululu, ndi midzi yonse yosungiramo chuma, imene anaimanga m'Hamati. Anamanganso Betehoroni wa kumtunda, ndi Betehoroni wa kunsi, midzi ya malinga yokhala nao malinga, zitseko, ndi mipiringidzo; ndi Baalati, ndi midzi yonse yosungiramo chuma anali nayo Solomoni, ndi midzi yonse ya magaleta ake, ndi midzi ya apakavalo ake, ndi zonse anazifuna Solomoni kuzimanga zomkondweretsa m'Yerusalemu, ndi m'Lebanoni, ndi m'dziko lonse la ufumu wake. Ndipo anthu onse otsala mwa Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, osati Aisraele, mwa ana ao otsala m'dziko pambuyo pao, amene ana a Israele sanawathe, mwa iwowa Solomoni anawachititsa thangata mpaka lero lino. Koma mwa ana a Israele Solomoni sanawayese akapolo omgwirira ntchito; koma iwowa anali anthu a nkhondo, akazembe ake akulu, ndi akulu a magaleta ake, ndi apakavalo ake. Amenewa anali akulu a akapitao a mfumu Solomoni, ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu akulamulira anthu. Ndipo Solomoni anamkweretsa mwana wamkazi wa Farao m'mudzi wa Davide, alowe m'nyumba imene adammangira; pakuti anati, Mkazi wanga asakhale m'nyumba ya Davide mfumu ya Israele; popeza mpopatulika pamene panafika likasa la Yehova. Pamenepo Solomoni anapereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa guwa la nsembe la Yehova, limene adalimanga pakhomo pachipinda cholowera, monga momwe mudayenera, tsiku ndi tsiku; napereka monga momwe adauza Mose pamasabata, pokhala mwezi, ndi pa zikondwerero zoikika, katatu m'chaka, pa zikondwerero za Mkate wopanda chotupitsa, ndi pa zikondwerero za Masabata, ndi pa zikondwerero za Misasa. Ndipo anaika monga mwa chiweruzo cha Davide atate wake zigawo za ansembe ku utumiki wao, ndi Alevi ku udikiro wao, kulemekeza Mulungu, ndi kutumikira pamaso pa ansembe, monga munayenera tsiku ndi tsiku; odikira omwe monga mwa zigawo zao ku chipata chilichonse; pakuti momwemo Davide munthu wa Mulungu adamuuza. Ndipo sanapatuke pa lamulo la mfumu la kwa ansembe ndi Alevi, kunena za kanthu kalikonse, kapena za chumachi. Momwemo ntchito yonse ya Solomoni inakonzekeratu tsiku lakuika maziko a nyumba ya Yehova, mpaka anaitsiriza. Pamenepo Solomoni anamuka ku Eziyoni-Gebere, ndi ku Eloti m'mphepete mwa nyanja, m'dziko la Edomu. Ndipo Huramu anamtumizira zombo, ndi amalinyero ake, ndi anyamata akudziwa za m'nyanja; ndipo anamuka pamodzi ndi anyamata a Solomoni ku Ofiri, natengako matalente mazana anai mphambu makumi asanu a golide, nabwera nao kwa Solomoni mfumu. Ndipo atamva mfumu yaikazi ya ku Sheba mbiri ya Solomoni, anadza kumuyesera Solomoni ndi miyambi yododometsa ku Yerusalemu, ndi ulendo waukulu, ndi ngamira zosenza zonunkhira, ndi golide wochuluka, ndi timiyala ta mtengo wake; ndipo atafika kwa Solomoni anakamba naye zonse za m'mtima mwake. Ndipo Solomoni anammasulira mau ake onse, panalibe kanthu kombisikira Solomoni, kamene sanammasulire. Ndipo mfumu yaikazi ya ku Sheba ataiona nzeru ya Solomoni, ndi nyumba adaimanga, ndi zakudya za pa gome lake, ndi makhalidwe a anyamata ake, ndi maimiriridwe a atumiki ake, ndi mavalidwe ao, ndi makweredwe ake pokwera iye kunka kunyumba ya Yehova, munalibenso moyo mwa iye. Ndipo anati kwa mfumu, Inali yoona mbiri ija ndidaimva m'dziko langa, ya machitidwe anu, ndi ya nzeru zanu. Koma sindinakhulupirira mau ao mpaka ndinadza, ndaona ndi maso anga; ndipo taonani anandifotokozera dera lina lokha la nzeru zanu zochuluka; mwaonjezatu pa mbiri ndidaimva. Odala anthu anu, ndi odala anyamata anu awa akuima chiimirire pamaso panu, ndi kumva nzeru zanu. Wolemekezeka Yehova Mulungu wanu, wakukondwera nanu, kukuikani pa mpando wachifumu wake, mukhalire Yehova Mulungu wanu mfumu pa anthu ake; popeza Mulungu wanu anakonda Aisraele kuwakhazika kosatha, anakulongani mfumu yao, kuchita chiweruzo ndi chilungamo. Ndipo mkaziyo anapatsa mfumu matalente a golide zana limodzi mphambu makumi awiri, ndi zonunkhira zambiri ndithu, ndi timiyala ta mtengo wake; panalibe zonunkhira zina zonga zija mfumu yaikazi ya ku Sheba anapatsa mfumu Solomoni. Ndiponso anyamata a Huramu, ndi anyamata a Solomoni otenga golide ku Ofiri, anatenga mitengo yambawa ndi timiyala ta mtengo wapatali. Ndipo mfumu inasema mitengo yambawa ikhale mizati ya nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi azeze, ndi zisakasa za oimbira; sizinaoneka zotere ndi kale lonse m'dziko la Yuda. Ndipo mfumu Solomoni anampatsa mfumu yaikazi ya ku Sheba chifuniro chake chonse, chilichonse anachipempha, osawerengera zija adabwera nazo kwa mfumu. Momwemo anabwerera, namuka ku dziko lake, iyeyu ndi anyamata ake. Kulemera kwake tsono kwa golide anafika kwa Solomoni chaka chimodzi ndiko matalente mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi limodzi a golide; osawerenga uja anabwera naye amalonda oyendayenda, ndi amalonda ena; ndipo mafumu onse a Arabiya, ndi akazembe a dziko, anadza naye golide ndi siliva kwa Solomoni. Ndipo mfumu Solomoni anapanga zikopa mazana awiri za golide wonsansantha, chikopa chimodzi chinathera golide wonsansantha masekeli mazana awiri. Napanganso malihawo mazana atatu a golide wonsansantha, chikopa chimodzi chinathera masekeli mazana atatu a golide; ndipo mfumu inazilonga m'nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni. Mfumu inapanganso mpando wachifumu waukulu wa minyanga, naukuta ndi golide woona. Ndi mpando wachifumuwo unali nao makwerero asanu ndi limodzi, ndi chopondapo mapazi chagolide, omangika ku mpandowo; ndi ku mbali zonse ziwiri za pokhalirapo kunali manja; ndi mikango iwiri inaimirira m'mbali mwa manjawo. Ndi mikango khumi ndi iwiri inaimirirapo, mbali ina ndi ina, pa makwerero asanu ndi limodzi; sanapangidwe wotere m'ufumu uliwonse. Ndipo zikho zomwera zonse za mfumu Solomoni zinali zagolide, ndi zipangizo zonse za nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni zinali za golide woona; siliva sanayesedwe kanthu m'masiku a Solomoni. Pakuti zombo za mfumu zinayenda ku Tarisisi ndi anyamata a Huramu; zombo za ku Tarisisi zinadza kamodzi zitapita zaka zitatu, ndi kubwera nazo golide, ndi siliva, minyanga, ndi apusi, ndi mbalame za zitsukwa zazitali za mawangamawanga. Momwemo mfumu Solomoni inaposa mafumu onse a pa dziko lapansi, kunena za chuma ndi nzeru. Ndipo mafumu onse a pa dziko lapansi anafuna nkhope ya Solomoni, kudzamva nzeru zake Mulungu adazilonga m'mtima mwake. Nabwera nao munthu yense mtulo wake, zipangizo zasiliva, ndi zipangizo zagolide, zovala, ndi zida za nkhondo, ndi mure, akavalo ndi nyuru; momwemo chaka ndi chaka. Ndipo Solomoni anali nazo zipinda zikwi zinai za akavalo ndi magaleta, ndi apakavalo zikwi khumi ndi ziwiri; nawaika m'midzi ya magaleta, ndi m'Yerusalemu kwa mfumu. Ndipo analamulira mafumu onse kuyambira ku Yufurate kufikira ku dziko la Afilisti, ndi ku malire a ku Ejipito. Ndipo mfumu inachulukitsa siliva m'Yerusalemu ngati miyala; ndi mikungudza anailinganiza ndi mikuyu ili kumadambo kuchuluka kwake. Ndipo anakamtengera Solomoni akavalo ku Ejipito, ndi ku maiko onse. Machitidwe ena tsono a Solomoni, oyamba ndi otsiriza, sanalembedwa kodi m'buku la mau a Natani mneneri ndi m'zonenera za Ahiya wa ku Silo, ndi m'masomphenya a Ido mlauli za Yerobowamu mwana wa Nebati? Ndipo Solomoni anakhala mfumu ya Israele yense m'Yerusalemu zaka makumi anai. Nagona Solomoni pamodzi ndi makolo ake, naikidwa m'mudzi wa Davide atate wake; ndipo Rehobowamu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake. Ndipo Rehobowamu anamuka ku Sekemu; pakuti Aisraele onse adadza ku Sekemu kumlonga ufumu. Ndipo kunali, atamva Yerobowamu mwana wa Nebati (popeza anali m'Ejipito kumene adathawira, kuthawa Solomoni mfumu), Yerobowamu anabwera kuchoka ku Ejipito. Ndipo anatuma munthu kukamuitana, nadza Yerobowamu ndi Aisraele onse, nalankhula ndi Rehobowamu, ndi kuti, Atate wanu analemeretsa goli lathu; inu tsono pepuzaniko ntchito yolemetsa ya atate wanu, ndi goli lake lolemera anatisenzetsali, ndipo tidzakutumikirani. Ndipo ananena nao, Mubwerenso atapita masiku atatu. Nachoka anthu. Ndipo Rehobowamu mfumu anafunsana ndi akuluakulu, amene anaimirira pamaso pa Solomoni atate wake akali ndi moyo, nati, Mundipangire bwanji, kuti ndiwabwezere mau anthu awa? Ndipo ananena naye, kuti, Mukawachitira chokoma anthu awa, ndi kuwakonda, ndi kulankhula nao mau okoma, adzakhala anyamata anu kosatha. Koma analeka uphungu wa akulu akuluwa adampangirawo, nakafunsana ndi anyamata anakula naye pamodzi, oimirira pamaso pake. Nati nao, Mundipangire bwanji inu, kuti tibwezere mau anthu awa ananena nanewo, ndi kuti, Mupepuze goli limene atate wanu anatisenzetsa ife? Ndipo anyamatawo adakula naye pamodzi ananena naye, ndi kuti, Muzitero nao anthu awa adalankhula nanu, ndi kuti, Atate wanu analemeretsa goli lathu, koma inu mutipepuzire ilo; muzitero nao, Kanense wanga adzaposa m'chuuno mwa atate wanga. Ndipo tsopano, popeza atate wanga anakusenzetsani goli lolemera, ine ndidzaonjezerapo pa goli lanu; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira. Tsono Yerobowamu ndi anthu onse anabwera kwa Rehobowamu tsiku lachitatu, monga mfumu idanena, ndi kuti Bweraninso kwa ine tsiku lachitatu. Ndipo mfumu inawayankha mokalipa, popeza mfumu Rehobowamu analeka uphungu wa akuluakulu, nalankhula nao monga umo anampangira achinyamata, ndi kuti, Atate wanga analemeretsa goli lanu, koma ine ndidzaonjezerapo; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira. Momwemo mfumu siinamvera anthuwo; pakuti kusinthaku kudafuma kwa Mulungu, kuti Yehova akhazikitse mau ake, amene ananenetsa Ahiya wa ku Silo kwa Yerobowamu mwana wa Nebati. Ndipo pakuona Aisraele onse kuti mfumu sinawamvera anthuwo, anamyankha mfumu, ndi kuti, Tili naye chiyani Davide? Inde tilibe cholowa m'mwana wa Yese; tiyeni kwathu, Aisraele inu; yang'anira nyumba yako tsopano, Davide. Momwemo Aisraele onse anamuka ku mahema ao. Koma za ana a Israele okhala m'midzi ya Yuda, Rehobowamu anakhalabe mfumu yao. Pamenepo Rehobowamu mfumu inatuma Hadoramu woyang'anira thangata; koma ana a Israele anamponya miyala, nafa. Ndipo Rehobowamu mfumu anafulumira kukwera pa galeta wake kuthawira ku Yerusalemu. Motero Israele anapandukana nayo nyumba ya Davide mpaka lero lino. Ndipo atafika ku Yerusalemu Rehobowamu, anamemeza a nyumba ya Yuda ndi Benjamini amuna osankhika zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu, ndiwo ankhondo, alimbane ndi Aisraele kubwezanso ufumu kwa Rehobowamu. Koma mau a Yehova anadza kwa Semaya munthu wa Mulunguyo, ndi kuti, Lankhula ndi Rehobowamu mwana wa Solomoni mfumu ya Yuda ndi Benjamini, ndi kuti, Atero Yehova, Musamuka kukayambana ndi abale anu, bwererani yense kunyumba yake; pakuti chinthu ichi chifuma kwa Ine. Ndipo anamvera mau a Yehova, nabwerera osakayambana ndi Yerobowamu. Ndipo Rehobowamu anakhala m'Yerusalemu, namanga midzi yolimbikiramo m'Yuda. Anamangadi Betelehemu, ndi Etamu, ndi Tekowa, ndi Betezuri, ndi Soko, ndi Adulamu, ndi Gati, ndi Maresa, ndi Zifi, ndi Adoraimu, ndi Lakisi, ndi Azeka, ndi Zora, ndi Ayaloni, ndi Hebroni; ndiyo midzi yamalinga ya m'Yuda ndi Benjamini. Ndipo analimbitsa malingawo, naikamo atsogoleri, ndi chakudya chosungikiratu, ndi mafuta, ndi vinyo. Ndi m'midzi iliyonse anaikamo zikopa ndi mikondo, nailimbitsa chilimbitsire. Ndipo Yuda ndi Benjamini anakhala ake. Ndipo ansembe ndi Alevi okhala m'Israele lonse anadziphatikiza kwa iye, ochokera m'malire ao onse. Pakuti Alevi anasiya podyetsa pao, ndi maiko aoao, nadza ku Yuda ndi ku Yerusalemu; popeza Yerobowamu ndi ana ake anawataya, kuti asachitire Yehova ntchito ya nsembe; nadziikira ansembe a misanje, ndi a ziwanda, ndi a anaang'ombe adawapanga. Ndipo akuwatsata iwo anadza ku Yerusalemu, ochokera m'mafuko onse a Israele, iwo akupereka mitima yao kufuna Yehova Mulungu wa Israele, kudzaphera Yehova Mulungu wa makolo ao nsembe. Momwemo analimbikitsa ufumu wa Yuda, nalimbikitsa Rehobowamu, mwana wa Solomoni zaka zitatu; pakuti anayenda m'njira ya Davide ndi Solomoni zaka zitatu. Ndipo Rehobowamu anadzitengera mkazi Mahalati, mwana wamkazi wa Yerimoti mwana wa Davide, ndi wa Abihaili mwana wamkazi wa Eliyabu mwana wa Yese; ndipo anambalira ana, Yeusi, ndi Semariya, ndi Zahamu. Ndi pambuyo pake anatenga Maaka mwana wamkazi wa Abisalomu; ndipo anambalira Abiya, ndi Atai, ndi Ziza, ndi Selomiti. Ndipo Rehobowamu anakonda Maaka mwana wamkazi wa Abisalomu koposa akazi ake onse, ndi akazi ake ang'ono (pakuti adatenga akazi khumi mphambu asanu ndi atatu, ndi akazi aang'ono makumi asanu ndi limodzi, nabala ana amuna makumi awiri mphambu asanu ndi atatu, ndi ana akazi makumi asanu ndi limodzi). Ndipo Rehobowamu anaika Abiya mwana wa Maaka akhale wamkulu, kalonga mwa abale ake; ndiko kuti adzamlonga ufumu. Ndipo anachita mwanzeru, nabalalitsa ana ake amuna onse m'maiko onse a Yuda ndi Benjamini, kumidzi yonse yamalinga; nawapatsa chakudya chochuluka, nawafunira akazi ochuluka. Ndipo kunachitika, utakhazikika ufumu wa Rehobowamu, nalimbika iye, anasiya chilamulo cha Yehova, ndi Aisraele onse pamodzi naye. Ndipo Rehobowamu atakhala mfumu zaka zinai, Sisake mfumu ya ku Ejipito anakwerera Yerusalemu, popeza iwo adalakwira Yehova. Anakwera ndi magaleta chikwi chimodzi mphambu mazana awiri, ndi apakavalo zikwi makumi asanu ndi limodzi, ndi anthu adadza naye kutuluka m'Ejipito ngosawerengeka, Alibiya, Asuki, ndi Akusi. Ndipo analanda midzi yamalinga yokhala ya Yuda, nadza ku Yerusalemu. Pamenepo Semaya mneneri anadza kwa Rehobowamu, ndi kwa akalonga a Yuda, atasonkhana ku Yerusalemu chifukwa cha Sisake, nati nao, Atero Yehova, Inu mwandisiya Ine, chifukwa chake Inenso ndasiya inu m'dzanja la Sisake. Pamenepo akalonga a Israele ndi mfumu anadzichepetsa, nati, Yehova ali wolungama. Ndipo pamene Yehova anaona kuti anadzichepetsa, mau a Yehova anadza kwa Semaya, ndi kuti, Anadzichepetsa; sindidzawaononga; koma katsala kanthawi ndipo ndidzawapatsa chipulumutso, wosatsanulira mkwiyo wanga pa Yerusalemu ndi dzanja la Sisake. Koma adzakhala akapolo ake, kuti adziwe kunditumikira kwanga, ndi kuwatumikira kwa maufumu a maiko. Ndipo Sisake mfumu ya Aejipito anakwerera Yerusalemu, nachotsa chuma cha m'nyumba ya Yehova, ndi chuma cha m'nyumba ya mfumu; anazichotsa zonse; anachotsanso zikopa zagolide adazipanga Solomoni. Ndipo Rehobowamu mfumu anapanga m'malo mwa izi zikopa zamkuwa, nazipereka m'manja mwa kapitao wa olindirira akusunga pakhomo pa nyumba ya mfumu. Ndipo kunatero kuti pakulowa mfumu m'nyumba ya Yehova, anadza olindirira, nazinyamula, nazibwezanso ku chipinda cha olindirira. Ndipo pakudzichepetsa iye mkwiyo wa Yehova unamchokera, kuti usamuononge konse; ndiponso munatsalira zokoma m'Yuda. Nadzilimbitsa Rehobowamu mfumu m'Yerusalemu, nachita ufumu; pakuti Rehobowamu anali wa zaka makumi anai mphambu chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri m'Yerusalemu, ndiwo mudzi Yehova adausankha m'mafuko onse a Israele, kuikapo dzina lake; ndipo dzina la make ndiye Naama Mwamoni. Koma anachita choipa, popeza sanalunjikitse mtima wake kufuna Yehova. Machitidwe ake tsono a Rehobowamu, zoyamba ndi zotsiriza, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a Semaya mneneriyo, ndi la Ido mlauliyo, lakunena za zibadwidwe? Ndipo panali nkhondo pakati pa Rehobowamu ndi Yerobowamu masiku onse. Nagona Rehobowamu ndi makolo ake, naikidwa m'mudzi wa Davide; ndipo Abiya mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake. Ndipo chaka chakhumi mphambu zisanu ndi zitatu cha Yerobowamu, Abiya analowa ufumu wa Yuda. Anakhala mfumu m'Yerusalemu zaka zitatu; ndi dzina la make ndiye Mikaya mwana wamkazi wa Uriyele wa ku Gibea. Ndipo panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobowamu. Ndipo Abiya anayambana nkhondo ali ndi khamu la ngwazi za nkhondo, amuna osankhika zikwi mazana anai; Yerobowamu atandandalitsa nkhondo yake ilimbane naye ndi amuna osankhika zikwi mazana asanu ndi atatu, ndiwo ngwazi zamphamvu. Ndipo Abiya anaimirira pa phiri la Zemaraimu, ndilo ku mapiri a Efuremu, nati, Mundimvere Yerobowamu ndi Aisraele onse; simudziwa kodi kuti Yehova Mulungu wa Israele anapereka chiperekere ufumu wa Israele kwa Davide, kwa iye ndi ana ake, ndi pangano lamchere? Koma Yerobowamu mwana wa Nebati mnyamata wa Solomoni mwana wa Davide anauka, napandukana ndi mbuye wake. Ndipo anamsonkhanira amuna achabe, anthu opanda pake, ndiwo anadzilimbikitsa kutsutsana naye Rehobowamu mwana wa Solomoni, muja Rehobowamu anali mnyamata ndi woolowa mtima, wosakhoza kuwalaka. Ndipo tsopano, mukuti mudzilimbikitse kutsutsana nao ufumu wa Yehova m'dzanja la ana a Davide; ndinu aunyinji ambiri, ndi pamodzi nanu anaang'ombe agolide adawapanga Yerobowamu akhale milungu yanu. Simunapirikitsa kodi ansembe a Yehova, ana a Aroni, ndi Alevi, ndi kudziikira ansembe monga amachita anthu a m'maiko ena? Kuti aliyense wakudza kudzipatulira ndi mwanawang'ombe, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri, yemweyo ndiye wansembe wa iyo yosati milungu. Koma ife, Yehova ndiye Mulungu wathu, sitinamsiya Iye; ndi ansembe tili nao akutumikira Yehova ana a Aroni, ndi Alevi, m'ntchito mwao, nafukizira Yehova nsembe zopsereza m'mawa ndi m'mawa, ndi madzulo onse, ndi zonunkhira za fungo lokoma, nakonza mkate woonekera pa gome lopatulika, ndi choikapo nyali chagolide ndi nyali zake, ziyake madzulo onse; pakuti tisunga chilangizo cha Yehova Mulungu wathu, koma inu mwamsiya Iye. Ndipo taonani, Mulungu ali nafe, wotitsogolera ndi ansembe ake, ndi malipenga oliza nao chokweza, kukulizirani inu chokweza. Ana a Israele inu, musalimbane naye Yehova Mulungu wa makolo anu; pakuti simudzapindula nako. Koma Yerobowamu anazunguliritsa owalalira, awadzere kumbuyo; momwemo iwowa anali kumaso kwa Yuda, ndi owalalira anali kumbuyo kwao. Ndipo pocheuka Yuda, taonani, nkhondo inayambana nao kumaso ndi kumbuyo; nafuulira iwo kwa Yehova, ndi ansembe analiza malipenga. Pamenepo amuna a Yuda anafuula chokweza; ndipo pofuula amuna a Yuda, kunachitika kuti Mulungu anakantha Yerobowamu ndi Aisraele onse pamaso pa Abiya ndi Yuda. Ndipo ana a Israele anathawa pamaso pa Yuda, nawapereka Mulungu m'dzanja lao. Ndipo Abiya ndi anthu ake anawakantha makanthidwe akulu; nagwa, nafa amuna osankhika zikwi mazana asanu a Israele. Momwemo anachepetsedwa ana a Israele nthawi ija, nalakika ana a Yuda; popeza anatama Yehova Mulungu wa makolo ao. Ndipo Abiya analondola Yerobowamu, namlanda midzi yake, Betele ndi milaga yake, ndi Yesana ndi milaga yake, ndi Efuroni ndi milaga yake. Ndi Yerobowamu sanaonenso mphamvu m'masiku a Abiya, namkantha Yehova, nafa iye. Koma Abiya anakula mphamvu, nadzitengera akazi khumi ndi anai, nabala ana amuna makumi awiri mphambu awiri, ndi ana akazi khumi mphamvu asanu ndi mmodzi. Machitidwe ena tsono a Abiya, ndi mayendedwe ake, ndi mau ake, alembedwa m'buku lomasulira la mneneri Ido. Momwemo Abiya anagona ndi makolo ake, ndipo anamuika m'mudzi wa Davide; ndi Asa mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake; m'masiku ake dziko linaona bata zaka khumi. Ndipo Asa anachita chokoma ndi choyenera m'maso mwa Yehova Mulungu wake, nachotsa maguwa a nsembe achilendo, ndi misanje; naphwanya zoimiritsa zao, nalikha zifanizo zao, nauza Yuda afune Yehova Mulungu wa makolo ao, ndi kuchita chilamulo ndi chowauza Iye. Anachotsanso m'midzi yonse ya Yuda misanje, ndi zifanizo za dzuwa; ndi ufumuwo unachita bata pamaso pake. Ndipo anamanga midzi yamalinga m'Yuda; pakuti dziko linachita bata, analibe nkhondo iyeyu zaka zija, popeza Yehova anampumulitsa. Ndipo anati kwa Yuda, Timange midzi iyi ndi kuizingira malinga, ndi nsanja, zitseko, ndi mipiringidzo; dziko likali pamaso pathu, popeza tafuna Yehova Mulungu wathu; tamfuna Iye, natipatsa mpumulo pozungulira ponse. Momwemo anamanga mosavutika. Ndipo Asa anali nao ankhondo ogwira zikopa ndi mikondo, a m'Yuda zikwi mazana atatu; ndi a m'Benjamini ogwira malihawo ndi okoka mauta zikwi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu; onsewo ngwazi zamphamvu. Ndipo anawatulukira Zera Mkusi ndi ankhondo zikwi chikwi chimodzi, ndi magaleta mazana atatu; nafika iye ku Maresa. Natuluka Asa pamaso pake, nanika nkhondoyi m'chigwa cha Zefati ku Maresa. Ndipo Asa anafuulira kwa Yehova Mulungu wake, nati, Yehova, palibe wina ngati Inu, kuthandiza pakati pa wamphamvu ndi iye wopanda mphamvu; tithandizeni Yehova Mulungu wathu, titama Inu, tatulukira aunyinji awa m'dzina lanu. Yehova, Inu ndinu Mulungu wathu, munthu asakukanikeni. Ndipo Yehova anakantha Akusi pamaso pa Asa ndi Yuda, nathawa Akusi. Ndi Asa ndi anthu anali naye anawalondola mpaka ku Gerari, nagwa Akusi ambiri osalimbikanso mphamvu iwowa; pakuti anathyoledwa pamaso pa Yehova ndi ankhondo ake; ndipo anatenga zofunkha zambiri. Ndipo anakantha midzi yonse pozungulira pake pa Gerari; pakuti mantha ochokera kwa Yehova anawagwera; ndipo anafunkha m'midzi monse, pakuti mudachuluka zofunkha m'menemo. Anakanthanso a m'mahema a ng'ombe, nalanda nkhosa zochuluka, ndi ngamira; nabwerera kunka ku Yerusalemu. Pamenepo mzimu wa Mulungu unagwera Azariya mwana wa Odedi, ndipo anatuluka kukomana naye Asa, nanena naye, Mundimvere, Asa, ndi onse Ayuda ndi Abenjamini, Yehova ali nanu; mukakhala ndi Iye, mukamfuna Iye, mudzampeza; koma mukamsiya, adzakusiyani. Masiku ambiri tsono Israele anakhala wopanda Mulungu woonayo, ndi wopanda wansembe wakuphunzitsa, ndi wopanda chilamulo; koma pamene anatembenukira kwa Yehova Mulungu wa Israele m'kusautsidwa kwao, ndi kumfuna, anampeza. Ndipo nthawi zija panalibe mtendere kwa iye wakutuluka, kapena kwa iye wakulowa, koma mavuto aakulu anagwera onse okhala m'maikomo. Ndipo anapasulidwa, mtundu wa anthu kupasula unzake, ndi mudzi kupasula mudzi; pakuti Mulungu anawavuta ndi masautso ali onse. Koma limbikani inu, manja anu asalende; pakuti ku ntchito yanu kuli mphotho. Ndipo pakumva Asa mau awa, ndi chinenero cha Odedi mneneriyo, analimbika mtima, nachotsa zonyansazo m'dziko lonse la Yuda ndi Benjamini, ndi m'midzi adailanda ku mapiri a Efuremu; nakonza guwa la nsembe la Yehova lokhala pakhomo pachipinda cholowera cha nyumba ya Yehova. Namemeza onse a m'Yuda ndi m'Benjamini, ndi iwo akukhala nao ochokera ku Efuremu, ndi Manase, ndi Simeoni; pakuti anamdzera ochuluka ochokera ku Israele, pamene anaona kuti Yehova Mulungu wake anali naye. Ndipo anasonkhana ku Yerusalemu mwezi wachitatu, Asa atakhala mfumu zaka khumi ndi zinai. Naphera Yehova nsembe tsiku lija za zofunkha adabwera nazo, ng'ombe mazana asanu ndi awiri, ndi nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri. Nalowa chipangano chakufuna Yehova Mulungu wa makolo ao ndi mtima wao wonse, ndi moyo wao wonse; ndi kuti yense wosafuna Yehova Mulungu wa Israele aphedwe, ngakhale wamng'ono kapena wamkulu, wamwamuna kapena wamkazi. Ndipo analumbira kwa Yehova ndi mau akulu, ndi kufuula ndi mphalasa ndi malipenga. Ndipo Yuda yense anakondwera nalo lumbirolo; pakuti adalumbira ndi mtima wao wonse, namfunafuna ndi chifuno chao chonse; ndipo anampeza; ndi Yehova anawapumulitsa pozungulirapo. Maaka yemwe, mai wake wa Asa, mfumu, namchotsa uyu asakhalenso mai wa ufumu, popeza anapanga fanizo lolaula; ndipo Asa analikha fanizolo, naliphwanyaphwanya, nalitenthera ku mtsinje wa Kidroni. Chinkana misanje siinachotsedwa m'Israele, mtima wa Asa unali wangwiro masiku ake onse. Ndipo analowa nazo zopatulika za atate wake, ndi zopatulika zakezake, kunyumba ya Mulungu; ndizo siliva, ndi golide, ndi zipangizo. Ndipo panalibenso nkhondo mpaka Asa atakhala mfumu zaka makumi atatu mphambu zinai. Chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi chimodzi cha Asa, Baasa mfumu ya Israele anakwera kulimbana ndi Yuda, namangitsa Rama, kuwaletsa anthu asatuluke kapena kulowa kwa Asa mfumu ya Yuda. Pamenepo Asa anatulutsa siliva ndi golide ku chuma cha nyumba ya Yehova, ndi cha nyumba ya mfumu; nazitumiza kwa Benihadadi mfumu ya Aramu, yokhala ku Damasiko, ndi kuti, Pakhale pangano pakati pa ine ndi inu, monga pakati pa atate wanga ndi atate wanu; taonani, ndakutumizirani siliva ndi golide; mukani, pasulani pangano lanu ndi Baasa mfumu ya Israele, kuti andichokere. Ndipo Benihadadi anamvera mfumu Asa natumiza akazembe a magulu ake a nkhondo ayambane ndi midzi ya Israele, nakantha Iyoni, ndi Dani, ndi Abele-Maimu, ndi midzi yonse ya chuma ya Nafutali. Ndipo kunali, pakumva ichi Baasa, analeka kumangitsa Rama, naleketsa ntchito yake. Pamenepo Asa mfumu anatenga Ayuda onse, ndipo anatuta miyala ya ku Rama, ndi mitengo yake, imene Baasa adamanga nayo, namangira Geba ndi Mizipa. Nthawi yomweyi Hanani mlauli anadza kwa Asa mfumu ya Yuda, nanena naye, Popeza mwatama mfumu ya Aramu, osatama Yehova Mulungu wanu, chifukwa chake khamu la nkhondo la mfumu ya Aramu lapulumuka m'dzanja lanu. Nanga Akusi ndi Alibiya, sanakhale khamu lalikulukulu, ndi magaleta ndi apakavalo ambirimbiri, koma muja munatama Yehova anawapereka m'dzanja mwanu? Pakuti maso a Yehova ayang'ana uko ndi uko m'dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wao uli wangwiro ndi Iye. Mwachita chopusa m'menemo; pakuti kuyambira tsopano mudzaona nkhondo. Koma Asa anakwiya naye mlauliyo, namuika m'kaidi; pakuti adapsa mtima naye chifukwa cha ichi. Nthawi yomweyi Asa anasautsa anthu ena. Ndipo taonani, zochita Asa, zoyamba ndi zotsiriza, zalembedwa m'buku la mafumu a Yuda ndi Israele. Ndipo Asa atakhala mfumu zaka makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu, anadwala nthenda ya mapazi, nikuladi nthendayi; koma podwala iye sanafune Yehova, koma asing'anga. Nagona Asa ndi makolo ake, namwalira atakhala mfumu zaka makumi anai. Ndipo anamuika m'manda ake adadzisemerawo m'mudzi wa Davide, namgoneka pa kama wodzala ndi zonunkhira za mitundumitundu, monga mwa makonzedwe a osanganiza; ndipo anampserezera zopsereza zambiri. Ndipo Yehosafati mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake, nadzilimbitsa kuyambana ndi Israele. Naika ankhondo m'midzi yonse yamalinga ya Yuda, naika aboma m'dziko la Yuda, ndi m'midzi ya Efuremu, imene adailanda Asa atate wake. Ndipo Yehova anali ndi Yehosafati, popeza anayenda m'njira zake zoyamba za kholo lake Davide, osafuna Abaala; koma anafuna Mulungu wa kholo lake nayenda m'malamulo ake, osatsata machitidwe a Israele. Chifukwa chake Yehova anakhazikitsa ufumuwo m'dzanja lake, ndi onse Ayuda anabwera nayo mitulo kwa Yehosafati; ndipo zidamchulukira chuma ndi ulemu. Ndi mtima wake unakwezeka m'njira za Yehova; anachotsanso misanje ndi zifanizo m'Yuda. Chaka chachitatu cha ufumu wake anatuma akalonga ake, ndiwo Benihayili, ndi Obadiya, ndi Zekariya, ndi Netanele, ndi Mikaya, aphunzitse m'midzi ya Yuda; ndi pamodzi nao Alevi, ndiwo Semaya, ndi Netaniya, ndi Zebadiya, ndi Asahele, ndi Semiramoti, ndi Yehonatani, ndi Adoniya, ndi Tobiya, ndi Tobadoniya, Alevi; ndi pamodzi nao Elisama ndi Yehoramu, ansembe. Ndipo anaphunzitsa m'Yuda ali nalo buku la chilamulo la Yehova, nayendayenda m'midzi yonse ya Yuda, naphunzitsa mwa anthu. Ndipo kuopsa kwa Yehova kunagwera maufumu a maiko ozungulira Yuda; momwemo sanayambane ndi Yehosafati. Ndipo Afilisti ena anabwera nazo kwa Yehosafati mitulo, ndi ndalama za msonkho; Aarabu omwe anabwera nazo kwa iye zoweta, nkhosa zamphongo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri ndi atonde zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri. Ndipo Yehosafati anakula chikulire, namanga m'Yuda nyumba zansanja, ndi midzi ya chuma. Nakhala nazo ntchito zambiri m'midzi ya Yuda, ndi anthu a nkhondo, ngwazi zamphamvu m'Yerusalemu. Kuwerenga kwao monga mwa nyumba za atate ao ndiko: a Yuda, akulu a zikwi; Adina wamkulu, ndi pamodzi ndi iye ngwazi zamphamvu zikwi mazana atatu; ndi wotsatana naye mkulu Yehohanani, ndi pamodzi ndi iye zikwi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu; ndi wotsatana naye Amasiya mwana wa Zikiri, wodzipereka kwa Yehova mwaufulu, ndi pamodzi ndi iye ngwazi zamphamvu zikwi mazana awiri; ndi a Benjamini: Eliyada ngwazi yamphamvu, ndi pamodzi ndi iye zikwi mazana awiri ogwira mauta ndi zikopa; wotsatana naye Yehozabadi, ndi pamodzi ndi iye okonzekeratu kunkhondo zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu. Ndiwo amene analindirira mfumu, osawerenga iwo aja mfumu adawaika m'midzi yamalinga m'Yuda monse. Yehosafati tsono anali nacho chuma ndi ulemu zomchulukira, nachita chibale ndi Ahabu. Ndipo zitatha zaka zina, anatsikira kwa Ahabu ku Samariya. Ndi Ahabu anamphera iye ndi anthu anali naye nkhosa, ndi ng'ombe zochuluka; namnyenga akwere naye pamodzi ku Ramoti Giliyadi. Nati Ahabu mfumu ya Israele kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, Mupita nane kodi ku Ramoti Giliyadi? Nayankha, nati, Monga inu momwemo ine; monga anthu anu momwemo anthu anga; tidzakhala nanu ku nkhondoyi. Ndipo Yehosafati anati kwa mfumu ya Israele, Funsiranitu mau a Yehova lero lino. Pamenepo mfumu ya Israele anamemeza aneneri amuna mazana anai, nanena nao, Kodi timuke kunkhondo ku Ramoti Giliyadi kapena ndileke? Ndipo anati, Kweraniko, pakuti Mulungu adzaupereka m'dzanja la mfumu. Koma Yehosafati anati, Kulibenso kuno mneneri wa Yehova, kuti tifunsire kwa iye? Ndipo mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Atsalanso munthu mmodzi, tifunsire Yehova kwa iye; koma ndimuda, pakuti sandinenera ine kanthu kokoma, koma zoipa nthawi zonse, ndiye Mikaya mwana wa Imila. Nati Yehosafati, Isatero mfumu. Pamenepo mfumu ya Israele inaitana mdindo, niti, Katenge msanga Mikaya mwana wa Imila. Mfumu ya Israele tsono ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakhala yense pa mpando wachifumu wake, ovala zovala zachifumu zao, nakhala pamalo popondera mphesa pakhomo pa chipata cha Samariya; ndi aneneri onse ananenera pamaso pao. Ndipo Zedekiya mwana wa Kenana anadzisulira nyanga zachitsulo, nati, Atero Yehova, Ndi izi udzagunda Aaramu mpaka adatha psiti. Ndi aneneri onse ananenera momwemo, ndi kuti, Kwerani ku Ramoti Giliyadi, mudzapindulako; pakuti Yehova adzaupereka m'dzanja la mfumu. Ndipo mthenga wakukaitana Mikaya ananena naye, ndi kuti, Taonani, mau a aneneri anenera mfumu chokoma ngati m'kamwa mmodzi; mau anu tsono akhaletu ngati amodzi a iwowa, nimunene chokoma. Nati Mikaya, Pali Yehova, chonena Mulungu wanga ndidzanena chomwechi. Pamene anafika kwa mfumu, mfumu inanena naye, Mikaya timuke ku Ramoti Giliyadi kunkhondo kodi, kapena ndileke? Nati iye, Kwerani, mudzachita mwai; ndipo adzaperekedwa m'dzanja lanu. Ndipo mfumu inati naye, Ndikulumbiritse kangati kuti unene nane choonadi chokhachokha m'dzina la Yehova? Nati iye, Ndinaona Aisraele onse obalalika pamapiri ngati nkhosa zopanda mbusa; nati Yehova, Awa alibe mbuye wao, abwerere yense kunyumba yake mumtendere. Ndipo mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Sindinakuuzani kuti sadzandinenera zabwino koma zoipa? Nati iye, Chifukwa chake tamvani mau a Yehova, Ndinaona Yehova alikukhala pa mpando wake wachifumu, ndi khamu lonse lakumwamba lilikuima pa dzanja lake lamanja, ndi pa dzanja lake lamanzere. Nati Yehova, Adzamnyenga Ahabu mfumu ya Israele ndani, kuti akwereko, nagwe ku Ramoti Giliyadi? Nati wina mwakuti, wina mwakuti. Ndipo unatuluka mzimu, nuima pamaso pa Yehova, nuti, Ndidzamnyenga ndine. Ndipo Yehova, ananena nao, Ndi chiyani? Nuti uwu, Ndidzatuluka ndi kukhala mzimu wonama m'kamwa mwa aneneri ake onse. Nati Iye, Udzamnyengadi, nudzakhoza; tuluka, ukatero kumene. Ndipo tsono taonani, Yehova analonga mzimu wabodza m'kamwa mwa aneneri anu awa, nakunenetserani choipa Yehova. Pamenepo Zedekiya mwana wa Kenana anayandikira, nampanda Mikaya patsaya, nati, Mzimu wa Yehova wandichokera bwanji kulankhula ndi iwe? Nati Mikaya, Tapenya, udzaona tsiku lolowa iwe m'chipinda cham'kati kubisala. Ndipo mfumu ya Israele inati, Mumtenge Mikaya, mukambweze kwa Amoni kazembe wa mudzi, ndi kwa Yowasi mwana wa mfumu; nimuziti, Itero mfumu, Mumuike uyu m'kaidi, ndi kumdyetsa chakudya chomsautsa, ndi kumwetsa madzi omsautsa, mpaka ndikabwera mumtendere. Nati Mikaya, Mukakabwera ndi mtendere konse, Yehova sananene mwa ine. Nati iye, Tamverani, anthu inu nonsenu. Momwemo mfumu ya Israele ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakwera kunka ku Ramoti Giliyadi. Ndi mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Ndidzadzizimbaitsa ndi kulowa kunkhondo, koma inu valani zovala zanu. Nidzizimbaitsa mfumu ya Israele, namuka iwo kunkhondo. Mfumu ya Aramu tsono idauza akapitao a magaleta ake, ndi kuti, Musayambana ndi ang'ono kapena akulu, koma ndi mfumu ya Israele yekha. Ndipo kunali, pamene akapitao a magaleta anaona Yehosafati, anati, Ndiye mfumu ya Israele. Potero anamtembenukira kuyambana naye; koma Yehosafati anafuula, namthandiza Yehova; ndipo Mulungu anawapatukitsa amleke. Ndipo kunali, pamene akapitao a magaleta anaona kuti sanali mfumu ya Israele anabwerera osamtsatanso. Ndipo munthu anaponya muvi wake chiponyeponye, nalasa mfumu ya Israeleyo pakati pa maluma a malaya ake achitsulo. Potero anati kwa woyendetsa galetayo, Tembenuza dzanja lako, nundichotse kukhamu la nkhondo kuno, pakuti ndalasidwa. Ndipo nkhondo inakula tsiku lija; koma mfumu ya Israele inagwirizizika m'galeta wake popenyana ndi Aaramu mpaka madzulo, namwalira nthawi yakulowa dzuwa. Ndipo Yehosafati mfumu ya Yuda anabwerera kunyumba yake ku Yerusalemu mumtendere. Natuluka Yehu mwana wa Hanani mlauli kukomana naye, nati kwa mfumu Yehosafati, Muyenera kodi kuthandiza zoipa, ndi kukonda amene adana ndi Yehova? Chifukwa cha ichi ukugwerani mkwiyo wochokera kwa Yehova. Koma zapezeka zokoma mwa inu, popeza mwazichotsa zifanizo m'dzikomo, mwalunjikitsanso mtima wanu kufuna Mulungu. Ndipo Yehosafati anakhala ku Yerusalemu, natulukiranso mwa anthu kuyambira ku Beereseba kufikira ku mapiri a Efuremu; nawabweza atsatenso Yehova Mulungu wa makolo ao. Naika oweruza m'dziko, m'midzi yonse yamalinga ya m'Yuda, mudzi ndi mudzi; nati kwa oweruza, Khalani maso umo muchitira; pakuti simuweruzira anthu koma Yehova; ndipo ali nanu Iyeyu pakuweruza mlandu. Ndipo tsono, kuopa Yehova kukhale pa inu, musamalire ndi kuchita; pakuti palibe chosalungama kwa Yehova Mulungu wathu, kapena kusamalira monga mwa nkhope ya munthu, kapena kulandira mphatso. Yehosafati anaikanso m'Yerusalemu Alevi, ndi ansembe ena, ndi akulu a nyumba za makolo m'Israele, aweruzire Yehova, nanena milandu. Ndipo anabwerera kudza ku Yerusalemu. Ndipo anawalangiza, ndi kuti, Muzitero ndi kuopa Yehova mokhulupirika ndi mtima wangwiro. Ndipo ukakudzerani mlandu uliwonse wochokera kwa abale anu okhala m'midzi mwao, kusiyanitsa pakati pa mwazi ndi mwazi, pakati pa chilamulo ndi chiuzo, malemba ndi maweruzo, muwachenjeze kuti asapalamule kwa Yehova, angafikitsire inu nokha ndi abale anu mkwiyo; muzitero, ndipo simudzapalamula. Ndipo taonani, Amariya wansembe wamkulu, ndiye mkulu wanu m'milandu yonse ya Yehova; ndi Zebadiya mwana wa Ismaele, wolamulira nyumba ya Yuda, m'milandu yonse ya mfumu; ndi Alevi akhale akapitao pamaso panu. Chitani molimbika mtima, ndipo Yehova akhale ndi abwino. Ndipo zitatha izi, kunachitika kuti ana a Mowabu, ndi ana a Amoni, ndi ena pamodzi ndi Aamoni, anadza kuyambana nkhondo ndi Yehosafati. Pamenepo anadza anthu akuuza Yehosafati, kuti, Ukudzerani unyinji waukulu wa anthu ochokera tsidya la nyanja ku Aramu; ndipo taonani, ali ku Hazazoni-Tamara, ndiwo Engedi. Ndipo Yehosafati anachita mantha, nalunjikitsa nkhope yake kufuna Yehova, nalalikira kusala mwa Ayuda onse. Namemezedwa Yuda afunsire kwa Yehova, inde anachokera kumidzi yonse ya Yuda kufuna Yehova. Ndipo Yehosafati anaima mu msonkhano wa Ayuda, ndi a ku Yerusalemu, kunyumba ya Yehova, pakati pa bwalo latsopano; nati, Yehova Mulungu wa makolo athu, Inu sindinu Mulungu wa m'Mwamba kodi? Sindinu woweruza maufumu onse a amitundu kodi? Ndi m'dzanja mwanu muli mphamvu yolimba; palibe wina wakulimbana ndi Inu. Sindinu Mulungu wathu, amene munainga nzika za m'dziko muno pa maso pa ana anu Israele, ndi kulininkha kwa mbeu ya Abrahamu bwenzi lanu kosatha? Nakhala m'mwemo iwowa, nakumangirani m'mwemo malo opatulika a dzina lanu, ndi kuti, Chikatigwera choipa, lupanga, chiweruzo, kapena mliri, kapena njala, tidzakhala chilili pakhomo pa nyumba iyi, ndi pamaso panu, (pakuti m'nyumba muno muli dzina lanu), ndi kufuulira kwa Inu m'kusauka kwathu; ndipo mudzamvera ndi kulanditsa. Ndipo tsopano, taonani ana a Amoni, ndi Mowabu, ndi a kuphiri la Seiri, amene simunalola Israele awalowere, pakutuluka iwo m'dziko la Ejipito, koma anawapatukira osawaononga; tapenyani, m'mene atibwezera, kudzatiinga m'cholowa chanu, chimene munatipatsa chikhale cholowa chathu. Mulungu wathu, simudzawaweruza? Pakuti mwa ife mulibe mphamvu yakulimbana nao aunyinji ambiri awa akutidzera; ndipo sitidziwa ngati tidzatani, koma maso athu ali kwa Inu. Ndipo Ayuda onse anakhala chilili pamaso pa Yehova, pamodzi ndi makanda ao, akazi ao, ndi ana ao. Pamenepo mzimu wa Yehova unagwera Yahaziele mwana wa Zekariya, mwana wa Benaya, mwana wa Yeiyele, mwana wa Mataniya, Mlevi, wa ana a Asafu, pakati pa msonkhano; nati iye, Tamverani Ayuda inu nonse, ndi inu okhala m'Yerusalemu, ndi inu mfumu Yehosafati, atero nanu Yehova, Musaope musatenge nkhawa chifukwa cha aunyinji ambiri awa; pakuti nkhondoyi si yanu, koma ya Mulungu. Mawa muwatsikire; taonani, akwera pokwerera pa Zizi, mudzakomana nao polekezera chigwa chakuno cha chipululu cha Yeruwele. Si kwanu kuchita nkhondo kuno ai; chilimikani, imani, nimupenye chipulumutso cha Yehova pa inu Yuda ndi Yerusalemu; musaope, kapena kutenga nkhawa; mawa muwatulukire, popeza Yehova ali ndi inu. Ndipo Yehosafati anawerama mutu wake, nkhope yake pansi; ndi Ayuda onse, ndi okhala m'Yerusalemu anagwa pansi pamaso pa Yehova, nalambira Yehova. Ndipo Alevi, a ana a Akohati, ndi a ana a Kora, anauka kulemekeza Yehova Mulungu wa Israele ndi mau omveketsa. Nalawira mamawa, natuluka kunka kuchipululu cha Tekowa; ndipo potuluka iwo, Yehosafati anakhala chilili, nati, Mundimvere ine, Ayuda inu, ndi inu okhala m'Yerusalemu, limbikani mwa Yehova Mulungu wanu, ndipo mudzakhazikika; khulupirirani aneneri ake, ndipo mudzalemerera. Ndipo atafunsana ndi anthu, anaika oimbira Yehova, ndi kulemekeza chiyero chokometsetsa, pakutuluka iwo kutsogolera khamu la nkhondo, ndi kuti, Yamikani Yehova, pakuti chifundo chake chikhala chosatha. Ndipo poyamba iwo kuimba, ndi kulemekeza Yehova, anaika olalira alalire Aamoni, Amowabu, ndi a m'phiri la Seiri, akudzera Ayuda; ndipo anawakantha. Pakuti ana a Amoni, ndi a Mowabu, anaukira okhala m'phiri la Seiri, kuwapha ndi kuwaononga psiti; ndipo atatha okhala m'Seiri, anasandulikirana kuonongana. Ndipo pofika Ayuda ku dindiro la kuchipululu, anapenyera aunyinjiwo; taonani, mitembo ili ngundangunda, wosapulumuka ndi mmodzi yense. Ndipo pofika Yehosafati ndi anthu ake kutenga zofunkha zao, anapezako chuma chambiri, ndi mitembo yambiri ndi zipangizo zofunika, nadzifunkhira, osakhoza kuzisenza zonse; nalimkutenga zofunkhazo masiku atatu, popeza zinachuluka. Ndi tsiku lachinai anasonkhana m'chigwa cha Beraka; pakuti pamenepo analemekeza Yehova; chifukwa chake anatcha dzina lake la malowo, Chigwa cha Beraka, mpaka lero lino. Pamenepo anabwerera amuna onse a Yuda, ndi a ku Yerusalemu, nawatsogolera ndi Yehosafati, kubwerera kunka ku Yerusalemu ndi chimwemwe; pakuti Yehova anawakondweretsa pa adani ao. Ndipo anafika ku Yerusalemu ndi zisakasa, ndi azeze, ndi malipenga, kunyumba ya Yehova. Ndipo kuopsa kwa Mulungu kunagwera maufumu onse a m'maiko, pamene anamva kuti Yehova adayambana ndi adani a Israele. Nuchita bata ufumu wa Yehosafati; pakuti Mulungu wake anampumulitsira pozungulirapo. Momwemo Yehosafati anakhala mfumu ya Yuda; anali wa zaka makumi atatu mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi awiri; ndi dzina la make ndiye Azuba mwana wa Sili. Ndipo anayenda m'njira ya Asa atate wake osapatukamo, nachita zoongoka pamaso pa Yehova. Komatu misanje siinachotsedwa; popeza pamenepo anthu sadakonzere mitima yao kwa Mulungu wa makolo ao. Machitidwe ena tsono adazichita Yehosafati, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zilembedwa m'buku la mau a Yehu mwana wa Hanani, wotchulidwa m'buku la mafumu a Israele. Zitatha izi, Yehosafati mfumu ya Yuda anaphatikana ndi Ahaziya mfumu ya Israele, yemweyo anachita moipitsitsa; naphatikana naye kupanga zombo zomuka ku Tarisisi, nazipanga zombozo m'Eziyoni-Gebere. Pamenepo Eliyezere mwana wa Dodavahu wa Maresa ananenera kumtsutsa Yehosafati, ndi kuti, Popeza waphatikana ndi Ahaziya Yehova wapasula ntchito zako. Ndipo zombo zinasweka zosakhoza kumuka ku Tarisisi. Ndipo Yehosafati anagona pamodzi ndi makolo ake, naikidwa pamodzi ndi makolo ake m'mudzi wa Davide; ndi Yehoramu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake. Ndipo anali nao abale ake, ana a Yehosafati, Azariya, ndi Yehiyele, ndi Zekariya, ndi Azariya, ndi Mikaele, ndi Sefatiya, onsewa ndiwo ana a Yehosafati mfumu ya Israele. Ndipo atate wao anawapatsa mphatso zazikulu, zasiliva, ndi zagolide, ndi za mtengo wake, pamodzi ndi midzi yamalinga m'Yuda; koma ufumu anauninkha kwa Yehoramu; pakuti ndiye mwana wake woyamba. Atauka tsono Yehoramu m'ufumu wa atate wake, nadzilimbitsa, anapha ndi lupanga abale ake onse, ndi akalonga ena omwe a Israele. Yehoramu anali wa zaka makumi atatu mphambu ziwiri polowa ufumu wake, nachita ufumu m'Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu. Nayenda m'njira ya mafumu a Israele, umo mwana wamkazi wa Ahabu anali mkazi wake; ndipo anachita choipa pamaso pa Yehova. Koma Yehova sanafune kuononga nyumba ya Davide chifukwa cha pangano adalichita ndi Davide, ndi monga adalonjeza kumpatsa iye ndi ana ake nyali nthawi zonse. Masiku ake Aedomu anapanduka kuchoka m'dzanja la Yuda, nadziponyera okha mfumu. Ndipo Yehoramu anaoloka, ndi akazembe ake, ndi magaleta ake onse pamodzi naye, nauka usiku, nakantha Aedomu omzinga ndi akapitao a magaleta. Chinkana anatero, Aedomu anapanduka kupulumuka m'dzanja la Yuda mpaka lero lino; nthawi yomweyo anapanduka Alibina kupulumuka m'dzanja lake; chifukwa adasiya Yehova Mulungu wa makolo ake. Anamanganso misanje m'mapiri a Yuda, nachititsa okhala m'Yerusalemu chigololo, nakankhirako Ayuda. Ndipo anamdzera kalata wofuma kwa Eliya mneneri, ndi kuti, Atero Yehova Mulungu wa Davide atate wanu, Popeza simunayenda m'njira za Yehosafati atate wanu, kapena m'njira za Asa mfumu ya Yuda, koma mwayenda m'njira ya mafumu a Israele, ndi kuchititsa Yuda ndi okhala m'Yerusalemu chigololo, monga umo anachitira chigololo a nyumba ya Ahabu, mwaphanso abale anu a nyumba ya atate wanu, ndiwo abwino akuposa inu; taonani, Yehova adzakantha anthu anu, ndi ana anu, ndi akazi anu, ndi chuma chanu chonse, makanthidwe akulu; ndipo mudzadwala kwakukulu nthenda yamatumbo, mpaka matumbo anu adzatuluka chifukwa cha nthendayi tsiku ndi tsiku. Ndipo Yehova anautsira Yehoramu mzimu wa Afilisti, ndi wa Aarabu okhala pambali pa Akusi; ndiwo anakwerera Yuda, nathyolamo, nalanda chuma chonse chinapezeka m'nyumba ya mfumu, ndi ana ake omwe, ndi akazi ake, osamsiyira mwana, koma Yehowahazi yekha mwana wake wamng'ono. Ndi pambuyo pake pa izi zonse Yehova anamdwalitsa m'matumbo ake ndi nthenda yosachira nayo. Ndipo kunali, itapita nthawi, pakutha pake pa zaka ziwiri, anatuluka matumbo ake mwa nthenda yake namwalira nazo nthenda zoipa. Ndipo anthu ake sanampserezere zonunkhira, monga umo anapserezera makolo ake. Anali wa zaka makumi atatu mphambu ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu, namuka wopanda wina womlakalaka; ndipo anamuika m'mudzi wa Davide, koma si m'manda a mafumu ai. Ndipo okhala m'Yerusalemu anamlonga Ahaziya mwana wake wamng'ono akhale mfumu m'malo mwake; pakuti gulu la anthu, adadzawo pamodzi ndi Aarabu kuchigono, adapha ana oyamba onse. Momwemo Ahaziya mwana wa Yehoramu anakhala mfumu ya Yuda. Ahaziya anali wa zaka makumi anai mphambu ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu chaka chimodzi; ndi dzina la make ndiye Ataliya mwana wa Omuri. Iyenso anayenda m'njira za nyumba ya Ahabu; pakuti wompangira ndi make achite choipa. Ndipo anachita choipa pamaso pa Yehova, monga umo anachitira a nyumba ya Ahabu; pakuti ompangira ndi iwowa, atamwalira atate wake; ndi kuonongeka kwake nkumeneko. Anayendanso m'kupangira kwao, namuka pamodzi ndi Yehoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Israele, kukayambana nkhondo ndi Hazaele mfumu ya Aramu ku Ramoti Giliyadi; ndipo Aaramu anamlasa Yehoramu. Nabwerera iye kuti amchize ku Yezireele, apole mabala amene adamkantha ku Rama, pamene anayambana ndi Hazaele mfumu ya Aramu. Ndipo Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anatsikira kukaona Yehoramu mwana wa Ahabu m'Yezireele, popeza anadwala. Kuonongeka kwa Ahaziya tsono nkwa Mulungu, kuti amuke kwa Yehoramu; pakuti atafika anatulukira pamodzi ndi Yehoramu kukayambana ndi Yehu mwana wa Nimisi, amene Yehova anamdzoza alikhe nyumba ya Ahabu. Ndipo kunali, pakulanga Yehu nyumba ya Ahabu, anapeza akalonga a Yuda, ndi ana a abale a Ahaziya, akutumikira Ahaziya, nawapha. Atatero, anafunafuna Ahaziya, namgwira alikubisala m'Samariya, nabwera naye kwa Yehu, namupha; ndipo anamuika; pakuti anati, Ndiye mwana wa Yehosafati, wofuna Yehova ndi mtima wake wonse. Ndipo panalibe wina wa nyumba ya Ahaziya wa mphamvu yakusunga ufumuwo. Pamene Ataliya mai wake wa Ahaziya anaona kuti mwana wake adafa, anauka, naononga mbeu yonse yachifumu ya nyumba ya Yuda. Koma Yehosabati mwana wamkazi wa mfumu anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, namuba pakati pa ana a mfumu ophedwa, namlonga iye ndi mlezi wake m'chipinda chogonamo. Momwemo Yehosabati mwana wamkazi wa mfumu Yehoramu, mkazi wa Yehoyada wansembe (popeza ndiye mlongo wake wa Ahaziya), anambisira Ataliya, angamuphe. Ndipo iye anali nao wobisika m'nyumba ya Mulungu zaka zisanu ndi chimodzi; nakhala Ataliya mfumu yaikazi ya dziko. Koma chaka chachisanu ndi chiwiri Yehoyada anadzilimbitsa natenga atsogoleri a mazana, Azariya mwana wa Yerohamu, ndi Ismaele mwana wa Yehohanani, ndi Azariya mwana wa Obedi, ndi Maaseiya mwana wa Adaya, ndi Elisafati mwana wa Zikiri, apangane naye pamodzi. Ndipo iwo anayendayenda mwa Yuda, nasonkhanitsa Alevi m'midzi yonse ya Yuda, ndi akulu a nyumba za makolo m'Israele; nadza iwo ku Yerusalemu. Ndipo msonkhano wonse unapangana pangano ndi mfumu m'nyumba ya Mulungu. Ndipo ananena nao, Taonani, mwana wa mfumu adzakhala mfumu monga Yehova ananena za ana a Davide. Chimene muzichita ndi ichi: limodzi la magawo atatu mwa inu olowera tsiku la Sabata, la ansembe ndi Alevi, akhale olindirira pakhomo; ndi limodzi la magawo atatu likhale kunyumba ya mfumu; ndi limodzi la magawo atatu ku Chipata cha Maziko; ndi anthu onse akhale m'mabwalo a nyumba ya Yehova. Koma asalowe mmodzi m'nyumba ya Yehova, ansembe okha, ndi Alevi otumikira, alowe iwowa; pakuti ndiwo opatulika; koma anthu onse asunge udikiro wa Yehova. Ndipo Alevi amzinge mfumu pozungulirapo, yense ndi zida zake m'dzanja mwake; ndipo aliyense wolowa m'nyumba aphedwe; nimukhale inu pamodzi ndi mfumu pakulowa ndi pakutuluka iye. Momwemo Alevi ndi Ayuda onse anachita monga mwa zonse anawauza Yehoyada wansembe; natenga yense amuna ake alowe tsiku la Sabata pamodzi ndi otuluka tsiku la Sabata; pakuti Yehoyada wansembe sanamasule zigawo. Ndi Yehoyada wansembe anapereka kwa akazembe a mazana mikondo, ndi zikopa, ndi malaya achitsulo, zinali za mfumu Davide, zokhala m'nyumba ya Mulungu. Ndipo anaika anthu onse, yense ndi chida chake m'dzanja lake, amzinge mfumu, kuyambira mbali ya kudzanja lamanja la nyumba kufikira mbali ya kudzanja lamanzere la nyumba, kuloza kuguwa la nsembe ndi kunyumba. Pamenepo anatulutsa mwana wa mfumu, namveka korona, nampatsa mboni, namlonga ufumu; ndi Yehoyada ndi ana ake anamdzoza, nati, Ikhale ndi moyo mfumu. Ndipo pamene Ataliya anamva phokoso la anthu alikuthamanga ndi kulemekeza mfumu, anadza kwa anthu m'nyumba ya Yehova; napenya, ndi kuona mfumu inaima pa nsanamira yake polowera; ndi atsogoleri, ndi malipenga, anali kwa mfumu; ndi anthu onse a m'dziko anakondwera, naomba amalipenga; oimbira omwe analiko ndi zoimbirazo, nalangiza poimbira cholemekeza. Pamenepo Ataliya anang'amba zovala zake, nati, Chiwembu, chiwembu. Koma Yehoyada wansembe anatuluka nao atsogoleri a mazana akuyang'anira khamu la nkhondo, nanena nao, Mtulutseni mkaziyo pakati pa mipambo; ndipo aliyense womtsata aphedwe ndi lupanga; pakuti wansembe adati, Msamphere m'nyumba ya Yehova. Ndipo anampisa malo; namuka iye kolowera ku Chipata cha Akavalo kunyumba ya mfumu; ndi pomwepo anamupha. Ndipo Yehoyada anachita pangano pakati pa iye, ndi anthu onse, ndi mfumu, kuti adzakhala anthu a Yehova. Ndi anthu onse anamuka kunyumba ya Baala, naipasula, naphwanya maguwa ake a nsembe, ndi mafano ake; namupha Matani wansembe wa Baala kumaguwa a nsembe. Ndipo Yehoyada anaika mayang'aniro a nyumba ya Yehova m'dzanja la ansembe Aleviwo, amene Davide anawagawa, ayang'anire nyumba ya Yehova; napereka nsembe zopsereza za Yehova monga mulembedwa m'chilamulo cha Mose, ndi kukondwera ndi kuimbira, monga mwa chilangizo cha Davide. Ndipo anaika odikira kumakomo a nyumba ya Yehova, kuti wodetsedwa nako kanthu kalikonse asalowemo. Natenga atsogoleri a mazana, ndi omveka, ndi akazembe a anthu, ndi anthu onse a m'dziko, natsika ndi mfumu kunyumba ya Yehova; nalowera pa chipata cha kumtunda m'nyumba ya mfumu, namkhalitsa mfumu pa mpando wa ufumu. Ndipo anthu onse a m'dziko anakondwera; ndi m'mudzi munali chete, atamupha Ataliya ndi lupanga. Yowasi anali wa zaka zisanu ndi ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi anai; ndi dzina la make ndiye Zibiya wa ku Beereseba. Ndipo Yowasi anachita zoongoka pamaso pa Yehova masiku onse a Yehoyada wansembe. Ndipo Yehoyada anamtengera akazi awiri, nabala ana aamuna ndi aakazi. Ndipo pambuyo pake mumtima mwa Yowasi munali chofuna kukonzanso nyumba ya Yehova. Nasonkhanitsa ansembe ndi Alevi, nanena nao, Mutuluke kunka kumidzi ya Yuda, ndi kusonkhanitsa kwa Aisraele onse ndalama zakukonzetsa nyumba ya Mulungu wanu chaka ndi chaka; ndipo inu fulumirani nayo ntchitoyi. Koma Alevi sanafulumire nayo. Ndipo mfumu inaitana Yehoyada mkulu wao, niti naye, Unalekeranji kuuza Alevi abwere nao kuchokera m'Yuda ndi Yerusalemu msonkho wa Mose mtumiki wa Yehova, ndi wa msonkhano wa Israele, ukhale wa chihema cha umboni? Pakuti ana a Ataliya mkazi woipa uja anathyola chitseko cha nyumba ya Mulungu, natenga zopatulidwa zonse za nyumba ya Yehova kuzipereka kwa Baala. Nilamulira mfumu, ndipo anapanga bokosi, naliika kunja kuchipata cha nyumba ya Yehova. Nalalikira mwa Yuda ndi Yerusalemu, abwere nao kwa Yehova msonkho umene Mose mtumiki wa Mulungu anauikira Aisraele m'chipululu. Ndipo akalonga onse ndi anthu onse anakondwera, nabwera nazo, naponya m'bokosi mpaka atatha. Ndipo kunali, pamene amabwera nalo bokosi alipenye mfumu, mwa manja a Alevi, nakapenya kuti ndalama zinachulukamo, amadza mlembi wa mfumu, ndi kapitao wa wansembe wamkulu, nakhuthula za m'bokosi, nalisenza ndi kubwera nalo kumalo kwake. Anatero tsiku ndi tsiku, nasonkhanitsa ndalama zochuluka. Ndipo mfumu ndi Yehoyada anazipereka kwa iwo akugwira ntchito ya utumiki ya nyumba ya Yehova, nalembera amisiri omanga ndi miyala, ndi osema mitengo, akonzenso nyumba ya Yehova; ndiponso akuchita ndi chitsulo ndi mkuwa alimbitse nyumba ya Yehova. Momwemo anachita ogwira ntchito, nikula ntchito mwa dzanja lao, nakhazikitsa iwo nyumba ya Mulungu monga mwa maonekedwe ake, nailimbitsa. Ndipo ataitsiriza, anabwera nazo ndalama zotsala kwa mfumu ndi Yehoyada, napanga nazo zipangizo za nyumba ya Yehova, zipangizo za kutumikira nazo, ndi kupereka nsembe nazo, ndi zipande, ndi zipangizo za golide ndi siliva. Ndipo anapereka kosalekeza nsembe zopsereza m'nyumba ya Yehova masiku onse a Yehoyada. Koma Yehoyada anakalamba, nachuluka masiku, namwalira iye; ndiye wa zaka zana limodzi mphambu makumi atatu pamene anamwalira. Ndipo anamuika m'mudzi wa Davide, pakati pa mafumu; pakuti anachita zabwino m'Israele, ndi kwa Mulungu, ndi kunyumba yake. Atamwalira Yehoyada tsono, akalonga a Yuda anadza, nalambira mfumu. Ndipo mfumu inawamvera. Ndipo anasiya nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo ao, natumikira zifanizo, ndi mafano; ndipo mkwiyo unawagwera Yuda ndi Yerusalemu, chifukwa cha kupalamula kwao kumene. Koma Iye anawatumira aneneri kuwabwezeranso kwa Yehova, ndiwo anawachitira umboni; koma sanawamvere. Ndipo mzimu wa Mulungu unavala Zekariya mwana wa Yehoyada wansembe, naima iye kumtunda kwa anthu, nanena nao, Atero Mulungu, Mulakwiranji malamulo a Yehova kuli kosalemerera nako? Popeza mwasiya Yehova, Iye wasiyanso inu. Koma anampangira chiwembu, namponya miyala, mwa lamulo la mfumu m'bwalo la nyumba ya Yehova. Motero mfumu Yowasi sanakumbukire zokoma anamchitirazi Yehoyada atate wake, koma anapha mwana wake; ndiye pomwalira anati, Yehova achipenye, nachifunse. Ndipo kunachitika, podzanso nyengoyi khamu la nkhondo la Aaramu linamkwerera, nafika iwo ku Yuda ndi Yerusalemu, naononga mwa anthu akalonga onse a anthu, natumiza zofunkha zao zonse kwa mfumu ya ku Damasiko. Pakuti khamu la nkhondo la Aaramu linadza la anthu owerengeka; ndipo Yehova anapereka khamu lalikulu m'dzanja lao; popeza adasiya Yehova Mulungu wa makolo ao. Motero anachitira Yowasi zomlanga. Ndipo atamchokera (popeza anamsiya wodwala nthenda zazikulu), anyamata ake anamchitira chiwembu, chifukwa cha mwazi wa ana a Yehoyada wansembe, namupha pakama pake, namwalira iye; ndipo anamuika m'mudzi wa Davide, koma osamuika m'manda a mafumu. Omchitira chiwembu ndi awa: Zabadi, mwana wa Simeati wamkazi Mwamoni; ndi Yehozabadi, mwana wa Simiriti wamkazi Mmowabu. Za ana ake tsono, ndi katundu wamkulu anamsenza, ndi kumanganso kwa nyumba ya Mulungu, taonani, zilembedwa m'buku lomasulira la mafumu. Ndipo Amaziya mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake. Amaziya anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai; ndi dzina la make ndiye Yehowadani wa ku Yerusalemu. Ndipo anachita zoongoka pamaso pa Yehova, koma wosachita ndi mtima wangwiro. Kunachitika tsono, utamkhazikikira ufumu, anapha anyamata ake amene adapha mfumu atate wake. Koma sanaphe ana ao, koma anachita monga umo mulembedwa m'chilamulo, m'buku la Mose, monga Yehova analamulira, ndi kuti, Atate asafere ana, ndi ana asafere atate; koma yense afere tchimo lakelake. Ndipo Amaziya anamemeza Ayuda, nawaika monga mwa nyumba za atate ao, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndiwo onse a Yuda ndi Benjamini; nawawerenga a zaka makumi awiri ndi mphambu, nawapeza amuna osankhika zikwi mazana atatu akutulukira kunkhondo, ogwira mkondo ndi chikopa. Analemberanso ngwazi zamphamvu za m'Israele zikwi zana limodzi, kuwalipira matalente a siliva zana limodzi. Koma anamdzera munthu wa Mulungu, kuti, Mfumu, khamu la nkhondo la Israele lisapite nanu; pakuti Yehova sakhala ndi Israele, sakhala ndi ana onse a Efuremu. Koma ngati mumuka, chitani, limbikani kunkhondo, Mulungu adzakugwetsani pamaso pa adani; pakuti Mulungu ali nayo mphamvu yakuthandiza ndi yakugwetsa. Ndipo Amaziya anati kwa munthu wa Mulungu, Koma nanga titani nao matalente zana limodzi ndinapatsa ankhondo a Israele? Nati munthu wa Mulungu, Yehova ali nazo zoposa izi kukupatsani. Pamenepo Amaziya anawapambutsa, ndiwo ankhondo anamdzera kuchokera ku Efuremu, amuke kwao; potero adapsa mtima kwambiri pa Yuda, nabwera kwao ndi kutentha mtima. Nalimbika mtima Amaziya. Natsogolera anthu ake, namuka ku Chigwa cha Mchere, nakantha ana a Seiri zikwi khumi. Ndi ana a Yuda anagwira zikwi khumi ena amoyo, nabwera nao pamwamba pa thanthwe, naphwanyika onsewo. Koma amuna a nkhondo amene Amaziya anawabwereretsa, kuti asamuke naye kunkhondo, anagwera midzi ya Yuda kuyambira Samariya kufikira Betehoroni, nakantha a iwowa zikwi zitatu, nalanda zofunkha zambiri. Ndipo kunali, atafika Amaziya atatha kuwapha Aedomu, ndi kubwera nayo milungu ya ana a Seiri, anaiika ikhale milungu yake, naigwadira, naifukizira. Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Amaziya, ndipo anamtumira mneneri amene anati, Mwafuniranji milungu ya anthu imene siinalanditsa anthu ao m'dzanja lanu? Ndipo kunali, pakulankhula naye mfumu, inanena naye, Takuika kodi ukhale wopangira mfumu? Leka, angakukanthe. Pamenepo mneneriyo analeka, nati, Ndidziwa kuti Mulungu watsimikiza mtima kukuonongani, popeza mwachita ichi ndi kusamvera kupangira kwanga. Pamenepo Amaziya mfumu ya Yuda anafunsana ndi ompangira, natumiza kwa Yowasi mwana wa Yehowahazi mwana wa Yehu mfumu ya Israele, ndi kuti, Idzani, tionane maso. Ndi Yowasi mfumu ya Israele anatumiza kwa Amaziya mfumu ya Yuda ndi kuti, Mtungwi wa ku Lebanoni unatumiza kwa mkungudza wa ku Lebanoni, ndi kuti, Mpatse mwana wanga wamwamuna mwana wako wamkazi akhale mkazi wake; koma nyama ya kuthengo ya ku Lebanoni inapitapo, nipondereza mtungwi. Mukuti, Taonani, ndakantha Aedomu, nukwezeka mtima wanu kudzikuza; khalani kwanu tsopano, mungadziutsire tsoka, mungagwe, inu, ndi Yuda pamodzi ndi inu. Koma wosamvera Amaziya, pakuti ncha Mulungu ichi kuti awapereke m'dzanja la adani ao; popeza anafuna milungu ya Edomu. Motero anakwera Yowasi mfumu ya Israele, ndipo iye ndi Amaziya mfumu ya Yuda anapenyana maso ku Betesemesi, ndiwo wa Yuda. Nakanthidwa Yuda pamaso pa Israele, nathawa yense kuhema kwake. Ndipo Yowasi mfumu ya Israele anagwira Amaziya mfumu ya Yuda, mwana wa Yowasi mwana wa Yehowahazi, ku Betesemesi, nabwera naye ku Yerusalemu, nagamula linga la Yerusalemu kuyambira chipata cha Efuremu kufikira chipata cha kungodya, mikono mazana anai. Natenga golide ndi siliva zonse, ndi zipangizo zonse zopezeka m'nyumba ya Mulungu kwa Obededomu, ndi chuma cha nyumba ya mfumu, achikole omwe; nabwerera kunka ku Samariya. Ndipo Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda anakhala ndi moyo, atamwalira Yowasi mwana wa Yehowahazi mfumu ya Israele, zaka khumi ndi zisanu. Machitidwe ena tsono a Amaziya, oyamba ndi otsiriza, taonani, sanalembedwa kodi m'buku la mafumu a Yuda ndi Israele? Ndipo chipatukire Amaziya kusatsata Yehova, namchitira chiwembu m'Yerusalemu, nathawira ku Lakisi iyeyu; koma anatuma omtsatira ku Lakisi, namupha komweko. Namnyamula pa akavalo, namuika pamodzi ndi makolo ake m'mudzi wa Yuda. Ndipo anthu onse Ayuda anatenga Uziya, ndiye wa zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi, namlonga ufumu m'malo mwa atate wake Amaziya. Iye anamanga Eloti, naubweza kwa Yuda, mfumuyo itagona ndi makolo ake. Uziya anali wa zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi asanu mphambu ziwiri; ndi dzina la make ndiye Yekoliya wa ku Yerusalemu. Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazichita atate wake Amaziya. Ndipo iye anali munthu wakufuna Mulungu masiku a Zekariya, ndiye wozindikira masomphenya a Mulungu; ndipo masiku akufunira Yehova iye, Mulungu anamlemereza; popeza anatuluka, nayambana ndi Afilisti, nagamula linga la Gati, ndi linga la Yabine, ndi linga la Asidodi; namanga midzi m'dziko la Asidodi, ndi mwa Afilisti. Ndipo Mulungu anamthandiza poyambana ndi Afilisti, ndi Aarabu okhala m'Guribaala, ndi Ameuni. Ndipo Aamoni anampatsa Uziya mitulo; ndi dzina lake linabuka mpaka polowera ku Ejipito; pakuti analimbika chilimbikire. Uziya anamanganso nsanja m'Yerusalemu pa chipata cha kungodya, ndi pa chipata cha kuchigwa, ndi popindika linga; nazilimbikitsa. Namanga nsanja m'chipululu, nakumba zitsime zambiri; popeza anali nazo zoweta zambiri; kumadambo, ndi kuzidikha; nakhala nao olima minda, ndi osunga mpesa kumapiri ndi kunthaka yopatsa bwino; pakuti anakonda kulima. Uziya anali nalonso khamu la anthu a nkhondo, otuluka kunkhondo magulu; nawawerenga monga mwa mawerengedwe ao ndi dzanja la mlembi Yeiyele, ndi kapitao Maaseiya, monga anawauza Hananiya kazembe wina wa mfumu. Chiwerengo chonse cha akulu a nyumba za makolo, ndiwo ngwazi zamphamvu, ndicho zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi limodzi. Ndipo m'dzanja mwao munali khamu la nkhondo zikwi mazana atatu mphambu zikwi zisanu ndi ziwiri kudza mazana asanu ochita nkhondo ndi mphamvu yaikulu, kuthandiza mfumu alimbane ndi adani. Ndipo Uziya anawakonzeratu ankhondo onse zikopa, ndi mikondo, ndi zisoti zachitsulo, ndi malaya achitsulo, ndi mauta, ndi miyala yoponyera. Napanga m'Yerusalemu makina, opangidwa ndi eni luso, akhale pansanja ndi kungodya, aponye nao mivi ndi miyala yaikulu. Ndi dzina lake linamveka kutali; pakuti anathandizidwa modabwitsa, mpaka analimbikatu. Koma atakhala wamphamvu, mtima wake unakwezeka momuononga, nalakwira Yehova Mulungu wake; popeza analowa m'Kachisi wa Yehova kufukiza pa guwa la nsembe la chofukiza. Ndipo Azariya wansembe analowa pambuyo pake, ndi pamodzi naye ansembe a Yehova makumi asanu ndi atatu, ndiwo olimba mtima; natsutsana ndi mfumu Uziya, nati kwa iye, Sikuyenera inu, Uziya, kufukizira Yehova koma ansembe, ana a Aroni opatulidwira kufukiza; tulukani m'malo opatulika; pakuti mwalakwa; Yehova Mulungu sakulemekezanipo. Koma Uziya anapsa mtima, mbale ya zofukiza ili m'dzanja lake kufukiza nayo; ndipo pakupsa mtima nao ansembe, khate linabuka pamphumi pake, pamaso pa ansembe m'nyumba ya Yehova, pambali pa guwa lofukizapo. Ndipo Azariya wansembe wamkulu, ndi ansembe onse, anampenya, ndi kuona kuti anali wakhate pamphumi pake namkankhira msanga kubwalo; nafulumiranso yekha kutulukako, pakuti Yehova adamkantha. Ndipo mfumu Uziya anali wakhate mpaka tsiku la imfa yake, nakhala m'nyumba ya padera, popeza ndiye wakhate; pakuti anadulidwa kunyumba ya Yehova; ndi Yotamu mwana wake anayang'anira nyumba ya mfumu naweruza anthu a m'dziko. Machitidwe ena tsono a Uziya, oyamba ndi otsiriza, anawalemba Yesaya mneneri mwana wa Amozi. Ndipo Uziya anagona ndi makolo ake, namuika ndi makolo ake kumanda kwa mafumu; pakuti anati, Ndiye wakhate; ndi Yotamu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake. Yotamu anali wa zaka makumi awiri, mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi; ndi dzina la make ndiye Yerusa mwana wa Zadoki. Ndipo anachita zoongoka pamaso pa Yehova, monga umo adachitira atate wake Uziya; pokhapo sanalowe m'Kachisi wa Yehova. Koma anthu anachitabe zovunda. Anamanga chipata cha kumtunda cha nyumba ya Yehova, ndi pa linga la Ofele anamanga kwakukulu. Namanga midzi m'mapiri a Yuda, ndi m'nkhalango anamanga nyumba zansanja, ndi nsanja zomwe. Anayambananso ndi mfumu ya ana a Amoni, namgonjetsa. Ndi ana a Amoni anamninkha chaka chomwechi matalente a siliva zana limodzi, ndi miyeso ya tirigu zikwi khumi, ndi ya barele zikwi khumi. Ana a Amoni anabwera nazo zomwezo kwa iye chaka chachiwiri ndi chachitatu chomwe. Momwemo Yotamu anakula mphamvu, popeza anakonza njira zake pamaso pa Yehova Mulungu wake. Machitidwe ena tsono a Yotamu, ndi nkhondo zake zonse, ndi njira zake, taonani, zalembedwa m'buku la mafumu a Israele ndi Yuda. Anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi. Ndipo Yotamu anagona ndi makolo ake, namuika m'mudzi wa Davide; ndi Ahazi mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake. Ahazi anali wa zaka makumi awiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi; koma sanachite zoongoka pamaso pa Yehova ngati Davide kholo lake, koma anayenda m'njira za mafumu a Israele, napangiranso Abaala mafano oyenga. Nafukizanso yekha m'chigwa cha mwana wa Hinomu, napsereza ana ake m'moto, monga mwa zonyansa za amitundu, amene Yehova anawainga pamaso pa ana a Israele. Naphera nsembe, nafukiza kumisanje, ndi kuzitunda, ndi patsinde pa mtengo uliwonse wogudira. Chifukwa chake Yehova Mulungu wake anampereka m'dzanja la mfumu ya Aramu; ndipo anamkantha, natenga ndende unyinji waukulu wa anthu ake, nafika nao ku Damasiko. Anaperekedwanso iye m'dzanja la mfumu ya Israele, amene anamkantha makanthidwe akulu. Pakuti Peka mwana wa Remaliya anapha ku Yuda tsiku limodzi zikwi zana limodzi ndi makumi awiri, ngwazi zonsezo; popeza adasiya Yehova Mulungu wa makolo ao. Ndipo Zikiri munthu wamphamvu wa Efuremu anapha Maaseiya mwana wa mfumu, ndi Azirikamu woyang'anira nyumba, ndi Elikana wotsatana ndi mfumu. Ndipo ana a Israele anatenga ndende ena a abale ao zikwi mazana awiri, akazi, ana aamuna ndi aakazi, nalandanso kwa iwo zofunkha zambiri, nabwera nazo zofunkhazo ku Samariya. Koma panali mneneri wa Yehova pomwepo, dzina lake Odedi; natuluka iye kukomana nayo nkhondo ikudzayo ku Samariya, nanena nao, Taonani, popeza Yehova Mulungu wa makolo anu anakwiya ndi Yuda, anawapereka m'dzanja lanu, nimunawapha ndi kupsa mtima kofikira kumwamba. Ndipo tsopano mukuti mugonjetse ana a Yuda ndi Yerusalemu akhale akapolo ndi adzakazi anu; palibe nanunso kodi milandu yopalamula kwa Yehova Mulungu wanu? Mundimvere tsono, bwezani andende a abale anu; pakuti mkwiyo waukali wa Yehova uli pa inu. Pamenepo akulu ena a ana a Efuremu, Azariya mwana wa Yohanani, Berekiya mwana wa Mesilemoti, ndi Yehizikiya mwana wa Salumu, ndi Amasa mwana wa Hadilai, anaukira aja ofuma kunkhondo, nanena nao, Musalowa nao andende kuno; pakuti inu mukuti mutipalamulitse kwa Yehova, kuonjezera pa machimo athu ndi zopalamula zathu; pakuti tapalamula kwakukulu, ndipo pali mkwiyo waukali pa Israele. Pamenepo eni zida anasiya andende ndi zofunkha pamaso pa akalonga msonkhano wonse. Nanyamuka amuna otchulidwa maina, natenga andende, naveka ausiwa onse mwa iwo ndi zofunkhazo, nawapatsa zovala, ndi nsapato, nawadyetsa ndi kuwamwetsa, nawadzoza, nasenza ofooka ao onse pa abulu, nafika nao ku Yeriko, mudzi wa migwalangwa, kwa abale ao; nabwerera iwo kunka ku Samariya. Nthawi yomweyo mfumu Ahazi anatumiza kwa mafumu a Asiriya amthandize. Pakuti Aedomu anadzanso, nakantha Yuda, natenga andende. Afilisti omwe adagwa m'midzi ya kuchidikha, ndi ya kumwera kwa Yuda, nalanda Betesemesi, ndi Ayaloni, ndi Gederoti, ndi Soko ndi milaga yake, ndi Timna ndi milaga yake, ndi Gimizo ndi milaga yake; nakhala iwo komweko. Pakuti Yehova anachepetsa Yuda chifukwa cha Ahazi mfumu ya Israele; popeza iye anachita chomasuka pakati pa Yuda, nalakwira Yehova kwambiri. Ndipo Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya anadza kwa iye, namsautsa osamlimbikitsa. Pakuti Ahazi analandako za m'nyumba ya Yehova ndi za m'nyumba ya mfumu, ndi ya akalonga, nazipereka kwa mfumu ya Asiriya, osathandizidwa nazo. Ndipo nthawi ya nsautso yake anaonjeza kulakwira Yehova, mfumu Ahazi yemweyo. Popeza anaphera nsembe milungu ya Damasiko yomkantha, nati, Popeza milungu ya mafumu a Aramu iwathandiza, ndiiphere nsembe, indithandize inenso. Koma inamkhumudwitsa iye, ndi Aisraele onse. Ndipo Ahazi anasonkhanitsa zipangizo za m'nyumba ya Mulungu, naduladula zipangizo za m'nyumba ya Mulungu, natseka pa makomo a nyumba ya Yehova, nadzimangira maguwa a nsembe m'ngodya zilizonse za Yerusalemu. Ndi m'midzi iliyonse ya Yuda anamanga misanje ya kufukizira milungu ina, nautsa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa makolo ake. Machitidwe ena tsono, ndi njira zake zonse, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zilembedwa m'buku la mafumu a Yuda ndi Israele. Ndi Ahazi anagona ndi makolo ake, namuika m'mudzi wa Yerusalemu; pakuti sanadze naye kumanda a mafumu a Israele; ndipo Hezekiya mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake. Hezekiya analowa ufumu wake ali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai; ndi dzina la make ndiye Abiya mwana wa Zekariya. Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga umo monse adachitira Davide kholo lake. Chaka choyamba cha ufumu wake, mwezi woyamba, anatsegula pa makomo a nyumba ya Yehova, napakonzanso. Nalowetsa ansembe ndi Alevi, nawasonkhanitsa pamaso poyera kum'mawa, nanena nao, Ndimvereni, Alevi inu, dzipatuleni, nimupatule nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo anu, ndi kuchotsa zoipsa m'malo opatulika. Pakuti analakwa makolo athu, nachita choipa pamaso pa Yehova Mulungu wathu, namsiya, natembenuza nkhope zao osapenya chokhalamo Yehova, namfulatira. Anatsekanso pa khomo chipinda cholowera, nazima nyalizo, osafukizanso zonunkhira kapena kupereka nsembe zopsereza m'malo opatulika kwa Mulungu wa Israele. Motero mkwiyo wa Yehova unali pa Yuda ndi Yerusalemu, nawapereka anjenjemere, nakhale chodabwitsa ndi chotsonyetsa, monga umo muonera m'maso mwanu. Pakuti taonani, makolo athu adagwa ndi lupanga, ndi ana athu aamuna ndi aakazi ndi akazi athu ali andende chifukwa cha ichi. Tsono mumtima mwanga nditi ndichite chipangano ndi Yehova Mulungu wa Israele, kuti mkwiyo wake waukali utembenuke kutichokera. Ana anga, musazengereza tsopano; popeza Yehova anakusankhani inu muime pamaso pake, kumtumikira Iye, ndi kuti mukhale atumiki ake ndi kufukiza zonunkhira. Pamenepo ananyamuka Alevi, Mahati mwana wa Amasai ndi Yowele mwana wa Azariya, a ana a Akohati; ndi a ana a Merari, Kisi mwana wa Abidi, ndi Azariya mwana wa Yehalelele; ndi a Ageresoni, Yowa mwana wa Zima, ndi Edeni mwana wa Yowa; ndi a ana a Elizafani, Simiri ndi Yeuwele; ndi a ana a Asafu, Zekariya ndi Mataniya; ndi a ana a Hemani, Yehuwele ndi Simei; ndi a ana a Yedutuni, Semaya ndi Uziyele. Ndipo anamemeza abale ao, nadzipatula, nalowa monga adawauza mfumu mwa mau a Yehova, kuyeretsa nyumba ya Yehova. Ndipo ansembe analowa m'kati mwake mwa nyumba ya Yehova kuiyeretsa, natulutsira kubwalo la nyumba ya Yehova zoipsa zonse anazipeza m'Kachisi wa Yehova. Nazilandira Alevi, kuzitulutsira kunja kumtsinje wa Kidroni. Anayamba tsono kuipatula tsiku loyamba la mwezi woyamba, nafikira kuchipinda cholowera cha nyumba ya Yehova tsiku lachisanu ndi chitatu la mwezi, naipatula nyumba ya Yehova m'masiku asanu ndi atatu; natsiriza tsiku lakhumi ndi chisanu ndi chimodzi. Pamenepo analowa m'katimo kwa mfumu Hezekiya, nati, Tayeretsa nyumba yonse ya Yehova, ndi guwa la nsembe yopsereza, ndi zipangizo zake zonse, ndi gome la mkate woonekera, ndi zipangizo zake zonse. Zipangizo zonse zomwe adazitaya mfumu Ahazi m'ufumu wake m'kulakwa kwake kuja, tazikonza, ndi kuzipatula; ndipo taonani, zili kuguwa la nsembe la Yehova. Pamenepo mfumu Hezekiya analawira mamawa, nasonkhanitsa akalonga a m'mudzi, nakwera kunka kunyumba ya Yehova. Ndipo anabwera nazo ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri ndi anaankhosa asanu ndi awiri, ndi atonde asanu ndi awiri, zikhale nsembe yauchimo ya ufumu, ndi ya malo opatulika, ndi ya Yuda. Ndipo anawauza ansembe ana a Aroni azipereke pa guwa la nsembe la Yehova. Momwemo anapha ng'ombezo, ndi ansembe analandira mwazi, nauwaza pa guwa la nsembe, napha nkhosa zamphongozo, nawaza mwazi pa guwa la nsembe; anaphanso anaankhosa aja, nawaza mwazi pa guwa la nsembe. Pamenepo anayandikiza nao atonde a nsembe yauchimo pamaso pa mfumu ndi msonkhano; ndipo iwo anawasanjika manja ao, ndi ansembewo anawapha, nachita nsembe yauchimo ndi mwazi wao pa guwa la nsembe, kuchita chotetezera Aisraele onse; pakuti mfumu idauza kuti nsembe yopsereza ndi nsembe yauchimo zikhale za Aisraele onse. Ndipo anaika Alevi m'nyumba ya Yehova ndi nsanje, ndi zisakasa, ndi azeze, monga umo adauzira Davide, ndi Gadi mlauli wa mfumu, ndi Natani mneneriyo; pakuti lamulo ili lidafuma kwa Yehova mwa aneneri ake. Alevi tsono anaimirira ndi zoimbira za Davide, ndi ansembe anakhala ndi malipenga. Nanena Hezekiya kuti apereke nsembe yopsereza pa guwa la nsembe. Ndipo pakuyamba nsembe yopsereza, inayambanso nyimbo ya Yehova ndi malipenga, pamodzi ndi zoimbira za Davideyo mfumu ya Israele. Ndi msonkhano wonse unalambira, ndi amalipenga anaomba; zonsezi mpaka adatsiriza nsembe yopsereza. Ndipo atatsiriza kuperekaku, mfumu ndi onse opezeka pamodzi naye anawerama, nalambira. Hezekiya mfumu ndi akalonga nauzanso Alevi aimbire Yehova zomlemekeza ndi mau a Davide ndi a Asafu mlauli. Ndipo anaimbira zomlemekeza mokondwera, nawerama mitu yao, nalambira. Pamenepo Hezekiya anayankha, nati, Tsopano mwadzipatulira kwa Yehova, senderani, bwerani nazo nsembe zophera ndi nsembe zoyamika kunyumba ya Yehova. Ndi msonkhano unabwera nazo nsembe zophera ndi nsembe zoyamika, ndi onse a mtima wofuna mwini anabwera nazo nsembe zopsereza. Ndi kuwerenga kwake kwa nsembe zopsereza unabwera nazo msonkhanowo ndiko ng'ombe makumi asanu ndi awiri, nkhosa zamphongo zana limodzi, ndi anaankhosa mazana awiri; zonsezi nza nsembe yopsereza ya Yehova. Ndi zinthu zopatulika zinafikira ng'ombe mazana asanu ndi limodzi, ndi nkhosa zikwi zitatu. Koma ansembe anaperewera, osakhoza kusenda nsembe zonse zopsereza; m'mwemo abale ao Alevi anawathandiza, mpaka idatha ntchitoyi, mpaka ansembe adadzipatula; pakuti Alevi anaposa ansembe m'kuongoka mtima kwao kudzipatula. Ndiponso zidachuluka nsembe zopsereza, pamodzi ndi mafuta a nsembe zamtendere, ndi nsembe zothira za nsembe yopsereza iliyonse. Momwemo utumiki wa nyumba ya Yehova unalongosoka. Nakondwera Hezekiya ndi anthu onse pa ichi Mulungu adakonzeratu; pakuti chinthuchi chidachitika modzidzimutsa. Ndipo Hezekiya anatumiza kwa Israele ndi Yuda onse, nalembanso akalata kwa Efuremu ndi Manase, kuti abwere kunyumba ya Yehova ku Yerusalemu, kuchitira Yehova Mulungu wa Israele Paska. Pakuti mfumu idapangana ndi akulu ake, ndi msonkhano wonse wa m'Yerusalemu, kuti achite Paska mwezi wachiwiri. Pakuti sanakhoze kumchita nthawi ija, popeza ansembe odzipatulira sanafikire, ndi anthu sadasonkhane ku Yerusalemu. Ndipo chinthuchi chinayenera m'maso mwa mfumu ndi msonkhano wonse. Motero anakhazikitsa mau kulalikira mwa Israele lonse, kuyambira Beereseba kufikira ku Dani, kuti abwere kuchitira Yehova Mulungu wa Israele Paska ku Yerusalemu; pakuti nthawi yaikulu sanachite monga mudalembedwa. Tsono amtokoma anamuka ndi akalata ofuma kwa mfumu ndi akulu ake mwa Israele ndi Yuda lonse, monga inauza mfumu ndi kuti, Inu ana a Israele, bwerani kwa Yehova Mulungu wa Abrahamu, Isaki, ndi Israele, kuti Iye abwere kwa otsala anu opulumuka m'dzanja la mafumu a Asiriya. Ndipo musamakhala ngati makolo anu ndi abale anu, amene analakwira Yehova Mulungu wa makolo ao, motero kuti anawapereka apasuke, monga mupenya. Musamakhala ouma khosi monga makolo anu; koma gwiranani dzanja ndi Yehova, nimulowe m'malo ake opatulika, amene anapatula kosatha, ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu; kuti mkwiyo wake waukali utembenuke kwa inu. Pakuti mukabwera kwa Yehova, abale anu ndi ana anu adzapeza chifundo; sadzakuyang'anirani kumbali ngati mubwera kwa Iye. Ndipo amtokoma anapitira m'midzi yonse ya dziko la Efuremu ndi Manase, mpaka Zebuloni; koma anawaseka pwepwete nawanyodola. Komatu ena a Asere ndi Manase ndi a Zebuloni anadzichepetsa, nadza ku Yerusalemu. Ku Yuda komwe kunali dzanja la Mulungu lakuwapatsa mtima umodzi, kuchita chowauza mfumu ndi akulu mwa mau a Yehova. Nasonkhana ku Yerusalemu anthu ambiri kuchita chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa mwezi wachiwiri, msonkhano waukulu ndithu. Ndipo anauka nachotsa maguwa a nsembe okhala m'Yerusalemu, nachotsa pofukizira zonunkhira, naziponya m'mtsinje wa Kidroni. Pamenepo anaphera Paska tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi wachiwiri, ndipo ansembe ndi Alevi anachita manyazi, nadzipatula, nabwera nazo nsembe zopsereza kunyumba ya Yehova. Naima m'malo mwao mwa kulongosoka kwao, monga mwa chilamulo cha Mose munthu wa Mulunguyo; ansembe anawaza mwazi, ataulandira kudzanja la Alevi. Pakuti munali ambiri mumsonkhano sanadzipatule; potero Alevi anayang'anira kupha za Paska kwa aliyense wosakhala woyera, kuwapatulira Yehova. Pakuti, anthu aunyinji, ndiwo ambiri a Efuremu, ndi Manase, Isakara, ndi Zebuloni, sanadziyeretse, koma anadya Paska mosati monga munalembedwa. Koma Hezekiya anawapempherera, ndi kuti, Yehova wabwino akhululukire yense wakuika mtima wake kufuna Mulungu Yehova, Mulungu wa makolo ake, chinkana sanayeretsedwe monga mwa mayeretsedwe a malo opatulika. Ndipo Yehova anamvera Hezekiya, nawachiritsa anthu. Ndipo ana a Israele opezeka m'Yerusalemu anachita chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri ndi chimwemwe chachikulu; ndi Alevi ndi ansembe analemekeza Yehova tsiku ndi tsiku ndi zoimbira zakuliritsa kwa Yehova. Ndipo Hezekiya ananena motonthoza mtima kwa Alevi onse akuzindikira bwino za utumiki wa Yehova. Ndipo anadya pamkomano masiku asanu ndi awiri, naphera nsembe zoyamika, ndi kulemekeza Yehova Mulungu wa makolo ao. Ndipo msonkhano wonse unapangana kuchita masiku asanu ndi awiri ena, nachita masiku asanu ndi ena ndi chimwemwe. Pakuti Hezekiya mfumu ya Yuda anapatsa msonkhano ng'ombe chikwi chimodzi, ndi nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri; ndi akulu anapatsa msonkhano ng'ombe chikwi chimodzi, ndi nkhosa zikwi khumi; ndipo ansembe ambiri adadzipatula. Ndi msonkhano wonse wa Yuda, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi, ndi msonkhano wonse wochokera kwa Israele, ndi alendo ochokera kudziko la Israele, ndi okhala m'Yuda, anakondwera. Momwemo munali chimwemwe chachikulu m'Yerusalemu; pakuti kuyambira masiku a Solomoni mwana wa Davide mfumu ya Israele simunachitika chotero m'Yerusalemu. Pamenepo ansembe Alevi anauka, nadalitsa anthu; ndi mau ao anamveka, ndi pemphero lao lidakwera pokhala pake popatulika Kumwamba. Chitatha ichi chonse tsono, Aisraele onse opezekako anatuluka kunka kumidzi ya Yuda, naphwanya zoimiritsa, nalikha zifanizo, nagamula misanje ndi maguwa a nsembe m'Yuda monse, ndi m'Benjamini, m'Efuremunso, ndi m'Manase, mpaka adaziononga zonse. Pamenepo ana onse a Israele anabwerera, yense kudziko lake ndi kumidzi yao. Ndipo Hezekiya anaika zigawo za ansembe ndi Alevi, monga mwa magawidwe ao, yense monga mwa utumiki wake, ndi ansembe ndi Alevi, achite nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika kutumikira, ndi kuyamika, ndi kulemekeza, kuzipata za chigono cha Ambuye. Naikanso gawo la mfumu lotapa pa chuma chake la nsembe zopsereza, ndilo la nsembe zopsereza za m'mawa ndi madzulo, ndi la nsembe zopsereza za masabata, ndi za pokhala mwezi, ndi za nyengo zoikika, monga mulembedwa m'chilamulo cha Yehova. Anauzanso anthu okhala m'Yerusalemu apereke gawo la ansembe ndi Alevi, kuti iwowa alimbike m'chilamulo cha Yehova. Ndipo pobuka mau aja, ana a Israele anapereka mochuluka, zobala zoyamba za tirigu, vinyo, ndi mafuta, ndi uchi, ndi za zipatso zonse za m'minda, ndi limodzi la magawo khumi la zonse anabwera nazo mochuluka. Ndi ana a Israele ndi Yuda okhala m'midzi ya Yuda, iwonso anabwera nalo limodzi la magawo khumi la ng'ombe, ndi nkhosa, ndi limodzi la magawo khumi la zinthu zopatulika, zopatulikira Yehova Mulungu wao; naziunjika miyulumiyulu. Mwezi wachitatu anayamba kuika miyalo ya miyuluyi, naitsiriza mwezi wachisanu ndi chiwiri. Ndipo pamene Hezekiya ndi akulu ake anadza, naona miyuluyi, analemekeza Yehova, nadalitsa anthu ake Aisraele. Pamenepo Hezekiya anafunsana ndi ansembe ndi Alevi za miyuluyi. Ndipo Azariya wansembe wamkulu wa nyumba ya Zadoki anamyankha, nati, Chiyambire anthu anabwera nazo zopereka kunyumba ya Yehova, tadya, takhuta, ndipo zitatsalira zambiri; pakuti Yehova anadalitsa anthu ake; ndipo siuku kuchuluka kwa chotsala. Pamenepo Hezekiya anawauza akonze zipinda m'nyumba ya Yehova; nazikonza. Ndipo anabwera nazo nsembe zokweza, ndi amodzi a magawo khumi, ndi zinthu zopatulika, mokhulupirika; ndi mkulu woyang'anira izi ndiye Konaniya Mlevi, ndi Simei mng'ono wake ndiye wotsatana naye. Ndi Yehiyele, ndi Azaziya, ndi Nahati, ndi Asahele, ndi Yerimoti, ndi Yozabadi, ndi Eliyele, ndi Isimakiya, ndi Mahati, ndi Benaya, ndiwo akapitao omvera Konaniya ndi Simei mng'ono wake, oikidwa ndi Hezekiya mfumu ndi Azariya mkulu wa kunyumba ya Mulungu. Ndipo Kore mwana wa Imina Mlevi, wa kuchipata cha kum'mawa, anayang'anira zopereka zaufulu za Mulungu, kugawira nsembe zokweza za Yehova, ndi zopatulika kwambiri. Ndi omvera iye ndiwo Edeni, ndi Miniyamini, ndi Yesuwa, ndi Semaya, Amariya ndi Sekaniya, m'midzi ya ansembe, kugawira abale ao m'zigawo zao mokhulupirika, akulu monga ang'ono; pamodzi ndi iwo oyesedwa mwa chibadwidwe cha amuna, kuyambira a zaka zitatu ndi mphambu, kwa aliyense amene adalowa m'nyumba ya Yehova, monga mwa ntchito yake pa tsiku lake, kukachita za utumiki wao m'udikiro wao monga mwa zigawo zao; ndi iwo oyesedwa mwa chibadwidwe cha ansembe mwa nyumba za makolo ao, ndi Alevi, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu m'udikiro mwao, monga mwa zigawo zao; ndi iwo oyesedwa mwa chibadwidwe cha ana ao ang'ono onse, akazi ao, ndi ana ao aamuna ndi aakazi, mwa msonkhano wonse; pakuti m'kukhulupirika kwao anadzipatula akhale opatulika; panalinso amuna mwa ana a Aroni ansembe, okhala m'minda ya kubusa kwa midzi yao, m'mudzi uliwonse, otchulidwa maina ao, agawire amuna onse mwa ansembe, ndi onse mwa Alevi, oyesedwa mwa chibadwidwe magawo ao. Momwemo anachita Hezekiya mwa Yuda lonse nachita chokoma, ndi choyenera, ndi chokhulupirika, pamaso pa Yehova Mulungu wake. Ndipo m'ntchito iliyonse anaiyamba m'utumiki wa nyumba ya Mulungu, ndi m'chilamulo, ndi m'mauzo, kufuna Mulungu wake, anachita ndi mtima wake wonse, nalemerera nayo. Zitatha zinthu izi zokhulupirika, anadza Senakeribu mfumu ya Asiriya, nalowera Yuda, namangira midzi yamalinga misasa, nati adzigonjetsere iyi. Ndipo pakuona Hezekiya kuti wadza Senakeribu, ndi kuti nkhope yake inalunjikitsa kuyambana nkhondo ndi Yerusalemu, anapangana ndi akulu ake ndi amphamvu ake, kutseka madzi a m'akasupe okhala kunja kwa mudzi; namthandiza iwo. Nasonkhana anthu ambiri, natseka akasupe onse, ndi mtsinje woyenda pakati pa dziko, ndi kuti, Angafike mafumu a Asiriya ndi kupeza madzi ambiri. Ndipo analimbika mtima, namangitsa linga lonse mopasuka, nalikweza mpaka pansanja, ndi linga lina kunja kwake, nalimbitsa Milo m'mudzi wa Davide, napanga zida ndi zikopa zochuluka. Naika akazembe a nkhondo alamulire anthu, nawasonkhanitsira kuli iye kubwalo la kuchipata cha mudzi, nanena nao motonthoza mtima wao ndi kuti, Limbani, mulimbike mtima, musaopa kapena kutenga nkhawa pankhope pa mfumu ya Asiriya ndi aunyinji okhala naye; pakuti okhala nafe achuluka koposa okhala naye; pamodzi ndi iye pali dzanja la thupi lanyama; koma pamodzi ndi ife pali Yehova Mulungu wathu, kutithandiza ndi kutigwirira nkhondo. Ndipo anthu anachirikizika ndi mau a Hezekiya mfumu ya Yuda. Pambuyo pake Senakeribu mfumu ya Asiriya, akali ku Lakisi ndi mphamvu yake yonse pamodzi naye, anatuma anyamata kwa Hezekiya mfumu ya Yuda, ndi kwa Ayuda onse okhala ku Yerusalemu, ndi kuti, Atero Senakeribu mfumu ya Asiriya, Mutama chiyani kuti mukhala m'linga m'Yerusalemu? Sakukopani Hezekiya, kuti akuperekeni mufe nayo njala ndi ludzu, ndi kuti, Yehova Mulungu wathu adzatilanditsa m'dzanja la mfumu ya Asiriya? Sanaichotse misanje yake ndi maguwa ake a nsembe Hezekiya yemweyo, nauza Yuda ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mugwadire kuguwa la nsembe limodzi ndi kufukiza zonunkhira pamenepo? Simudziwa kodi chomwe ine ndi makolo anga tachitira anthu onse a m'maikomo? Kodi milungu ya mitundu ya anthu inakhoza konse kulanditsa dziko lao m'dzanja langa? Ndi uti mwa milungu yonse ya mitunduyi ya anthu, amene makolo anga anawaononga konse, unakhoza kulanditsa anthu ake m'dzanja mwanga? Ndipo tsono, asakunyengeni Hezekiya, ndi kukukopani motero, musamkhulupirira; pakuti palibe Mulungu wa mtundu uliwonse wa anthu, kapena ufumu uliwonse, unakhoza kulanditsa anthu ake m'dzanja mwanga; ndipo kodi Mulungu wanu adzakulanditsani inu m'dzanja langa? Ndipo anyamata ake anaonjeza kunena motsutsana ndi Yehova Mulungu, ndi mnyamata wake Hezekiya. Analemberanso akalata a kunyoza Yehova Mulungu wa Israele, ndi kunena motsutsana ndi Iye, ndi kuti, Monga milungu ya mitundu ya anthu a m'maiko, imene siinalanditsa anthu ao m'dzanja langa, momwemo Mulungu wa Hezekiya sadzalanditsa anthu ake m'dzanja mwanga. Ndipo anafuula ndi mau akulu m'chinenedwe cha Ayuda kwa anthu a m'Yerusalemu okhala palinga, kuwaopsa ndi kuwavuta, kuti alande mudziwu. Nanenera Mulungu wa Yerusalemu, monga umo amanenera milungu ya mitundu ya anthu a pa dziko lapansi, ndiyo ntchito ya manja a anthu. Ndipo Hezekiya mfumu, ndi Yesaya mneneri mwana wa Amozi, anapemphera pa ichi, nafuulira Kumwamba. Ndipo Yehova anatuma wamthenga amene anaononga ngwazi zamphamvu zonse, ndi atsogoleri, ndi akazembe, kuchigono cha mfumu ya Asiriya. Nabwerera iye ndi nkhope yamanyazi kudziko lake. Ndipo atalowa m'nyumba ya mulungu wake, iwo otuluka m'matumbo mwake anamupha ndi lupanga pomwepo. Momwemo Yehova analanditsa Hezekiya ndi okhala m'Yerusalemu m'dzanja la Senakeribu mfumu ya Asiriya, ndi m'dzanja la onse ena, nawatsogolera monsemo. Ndipo ambiri anabwera nayo mitulo kwa Yehova ku Yerusalemu, ndi za mtengo wake, kwa Hezekiya mfumu ya Yuda; nakwezeka iye pamaso pa amitundu onse kuyambira pomwepo. Masiku omwe aja Hezekiya anadwala pafupi imfa; ndipo anapemphera kwa Yehova; ndi Iye ananena naye, nampatsa chizindikiro chodabwitsa. Koma Hezekiya sanabwezere monga mwa chokoma anamchitira, pakuti mtima wake unakwezeka; chifukwa chake unamdzera mkwiyo iye, ndi Yuda, ndi Yerusalemu. Koma Hezekiya anadzichepetsa m'kudzikuza kwa mtima wake, iye ndi okhala m'Yerusalemu, momwemo mkwiyo wa Yehova sunawadzera masiku a Hezekiya. Ndipo chuma ndi ulemu zinachulukira Hezekiya, nadzimangira iye zosungiramo siliva, ndi golide, ndi timiyala ta mtengo wake, ndi zonunkhira, ndi zikopa, ndi zipangizo zokoma zilizonse; ndi nyumba zosungiramo zipatso za tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi zipinda za nyama iliyonse, ndi makola a zoweta. Nadzimangiranso midzi, nadzionera nkhosa ndi ng'ombe zochuluka; pakuti Mulungu adampatsa chuma chambirimbiri. Hezekiya yemweyo anatseka kasupe wa kumtunda wa madzi a Gihoni, nawapambutsa atsikire kumadzulo kwa mudzi wa Davide. Ndipo Hezekiya analemerera nazo ntchito zake zonse. Koma pokhala naye akazembe a akalonga a ku Babiloni, amene anatumiza kwa iye kufunsira za chodabwitsa chija chidachitika m'dzikomo, Mulungu anamsiya, kumuyesa, kuti adziwe zonse za mumtima mwake. Machitidwe ena tsono a Hezekiya, ndi ntchito zake zokoma, taonani, zilembedwa m'masomphenya a Yesaya mneneri mwana wa Amozi, ndi m'buku la mafumu a Yuda ndi Israele. Ndipo Hezekiya anagona ndi makolo ake, namuika polowerera kumanda a ana a Davide; ndi Ayuda onse ndi okhala m'Yerusalemu anamchitira ulemu pa imfa yake. Ndipo Manase mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake. Manase anali wa zaka khumi ndi ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi asanu mphambu zisanu. Nachita choipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonyansa za amitundu, amene Yehova anawachotsa m'dziko mwao pamaso pa ana a Israele. Pakuti anamanganso misanje adaipasula Hezekiya atate wake, nautsira Abaala maguwa a nsembe, napanga zifanizo, nalambira khamu lonse la kuthambo, nalitumikira. Namanga maguwa a nsembe m'nyumba ya Yehova, imene Yehova adati, M'Yerusalemu mudzakhala dzina langa kunthawi zonse. Namangiranso khamu lonse la kuthambo maguwa a nsembe m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehova. Anapititsanso ana ake pamoto m'chigwa cha ana a Hinomu, naombeza maula, nasamalira malodza, nachita zanyanga, naika obwebweta ndi openduza; anachita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wake. Ndipo anaika chifanizo chosema cha fanolo adachipanga m'nyumba ya Mulungu, imene Mulungu adati kwa Davide ndi Solomoni mwana wake, M'nyumba muno ndi m'Yerusalemu umene ndausankha m'mafuko onse a Israele ndidzaika dzina langa kunthawi zonse; ndipo sindidzasunthanso phazi la Israele kudziko ndaliikira makolo anu; pokhapo asamalire kuchita zonse ndawalamulira, chilamulo chonse, ndi malemba, ndi maweruzo, mwa dzanja la Mose. Koma Manase analakwitsa Yuda ndi okhala m'Yerusalemu, kotero kuti anachita choipa koposa amitundu, amene Yehova anawaononga pamaso pa ana a Israele. Ndipo Yehova analankhula ndi Manase ndi anthu ake, koma sanasamalire. Motero Yehova anawafikitsira akazembe a khamu la nkhondo la mfumu ya Asiriya, namgwira Manase ndi zokowera, nammanga matangadza, namuka naye ku Babiloni. Ndipo popsinjika iye anapembedza Yehova Mulungu wake, nadzichepetsa kwambiri pamaso pa Mulungu wa makolo ake. Anampempha, ndipo anapembedzeka, namvera kupembedza kwake, nambwezera ku Yerusalemu m'ufumu wake. Pamenepo anadziwa Manase kuti Yehova ndiye Mulungu. Chitatha ichi tsono iye anaumangira mudzi wa Davide linga lakunja, kumadzulo kwa Gihoni, m'chigwa, mpaka polowera pa chipata chansomba; nazinga Ofele, nalikweza kwambiri; anaikanso akazembe a nkhondo m'midzi yonse yamalinga ya m'Yuda. Ndipo anachotsa milungu yachilendo, ndi fanoli m'nyumba ya Yehova, ndi maguwa onse a nsembe anawamanga m'phiri la nyumba ya Yehova ndi m'Yerusalemu, nawataya kunja kwa mudzi. Namanga guwa la nsembe la Yehova, napherapo nsembe zamtendere ndi zoyamika, nalamulira Yuda atumikire Yehova Mulungu wa Israele. Koma anthu anapherabe nsembe pamisanje; koma anaziphera Yehova Mulungu wao. Machitidwe ena tsono a Manase, ndi pemphero lake kwa Mulungu wake, ndi mau a alauli akunena naye m'dzina la Yehova Mulungu wa Israele, taonani, zalembedwa m'machitidwe a mafumu a Israele. Pemphero lake lomwe, ndi m'mene Mulungu anapembedzeka naye, ndi tchimo lake lonse, ndi kulakwa kwake, ndi apo anamanga misanje, naimika zifanizo ndi mafano osema asanadzichepetse, taonani, zalembedwa m'buku la mau a Hozai. Momwemo Manase anagona ndi makolo ake, namuika m'nyumba mwakemwake; ndi Amoni mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake. Amoni ndiye wa zaka makumi awiri mphambu ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka ziwiri. Ndipo anachita choipa pamaso pa Yehova, monga umo anachitira Manase atate wake; pakuti Amoni anaphera nsembe mafano osema onse amene adawapanga Manase atate wake, nawatumikira. Koma sanadzichepetse pamaso pa Yehova, monga umo anadzichepetsera Manase atate wake; koma Amoni amene anachulukitsa kupalamula kwake. Ndipo anyamata ake anampangira chiwembu, namupha m'nyumba yakeyake. Koma anthu a m'dziko anapha onse adampangira chiwembu mfumu Amoni; ndi anthu a m'dziko analonga Yosiya mwana wake akhale mfumu m'malo mwake. Yosiya ndiye wa zaka zisanu ndi zitatu polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi atatu mphambu chimodzi. Nachita zoongoka pamaso pa Yehova, nayenda m'njira za Davide kholo lake, osapatuka kudzanja lamanja kapena kulamanzere. Pakuti atakhala mfumu zaka zisanu ndi ziwiri akali mnyamata, anayamba kufuna Mulungu wa Davide kholo lake; ndipo atakhala zaka khumi ndi chimodzi anayamba kuyeretsa Yuda ndi Yerusalemu, kuzichotsa misanje, ndi zifanizo, ndi mafano osema, ndi mafano oyenga. Ndipo anthu anagumula maguwa a nsembe a Abaala pamaso pake; nawalikha mafano a dzuwa anakwezeka pamwamba pao; naphwanya zifanizo, ndi mafano osema, ndi mafano oyenga; nazipera, naziwaza pamanda pa iwo amene adaziphera nsembe. Napsereza mafupa a ansembe pa maguwa a nsembe ao, nayeretsa Yuda ndi Yerusalemu. Nateronso m'midzi ya Manase, ndi Efuremu, ndi Simeoni, mpaka Nafutali, m'mabwinja mwao mozungulira. Nagumula maguwa a nsembe, naperapera zifanizo ndi mafano osema, nalikha mafano a dzuwa onse m'dziko lonse la Israele, nabwerera kunka ku Yerusalemu. Atakhala mfumu tsono zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri, atayeretsa dziko ndi nyumbayi, anatuma Safani mwana wa Azaliya, ndi Maaseiya kazembe wa mudzi, ndi Yowa mwana wa Yehowahazi wolemba mbiri, akonze nyumba ya Yehova Mulungu wake. Ndipo anadza kwa Hilikiya mkulu wa ansembe, napereka ndalama adabwera nazo kunyumba ya Mulungu, zimene Alevi osunga pakhomo adasonkhanitsa kuzilandira kudzanja la Manase ndi Efuremu, ndi kwa otsala onse a Israele, ndi kwa Yuda yense, ndi Benjamini, ndi kwa okhala m'Yerusalemu. Ndipo anazipereka m'dzanja la antchito oikidwa ayang'anire nyumba ya Yehova; ndi iwo anazipereka kwa antchito akuchita m'nyumba ya Yehova kukonza ndi kulimbitsa nyumbayi; anazipereka kwa amisiri a mitengo ndi omanga nyumba, agule miyala yosema, ndi mitengo ya mitanda yam'mwamba ndi yammunsi ya nyumbazi, adaziononga mafumu a Yuda. Ndipo amunawo anachita ntchitoyi mokhulupirika; ndi oikidwa awayang'anire ndiwo Yahati ndi Obadiya, Alevi, a ana a Merari; ndi Zekariya ndi Mesulamu, a ana a Akohati, kuifulumiza; ndi Alevi ena aliyense waluso la zoimbira. Anayang'aniranso osenza akatundu, nafulumiza onse akugwira ntchito ya utumiki uliwonse; ndi mwa Alevi munali alembi, ndi akapitao, ndi odikira. Ndipo pakutulutsa ndalama zimene adalowa nazo kunyumba ya Yehova, Hilikiya wansembe anapeza buku la chilamulo la Yehova mwa dzanja la Mose. Ndipo Hilikiya anayankha nati kwa Safani mlembi, Ndapeza buku la chilamulo m'nyumba ya Yehova. Hilikiya napereka buku kwa Safani. Ndi Safani anamuka nalo buku kwa mfumu, nabwezeranso mau kwa mfumu, ndi kuti, Zonse mudazipereka kwa anyamata anu alikuzichita. Nakhuthula ndalama zinapezeka m'nyumba ya Yehova, nazipereka m'manja a akapitao ndi m'manja a antchito. Ndipo Safani mlembi anauza mfumu, ndi kuti, Hilikiya wansembe anandipatsa buku. Nawerengamo Safani pamaso pa mfumu. Ndipo kunali, atamva mfumu mau a chilamulo, anang'amba zovala zake. Mfumu niuza Hilikiya, ndi Ahikamu mwana wa Safani, ndi Abidoni mwana wa Mikaya, ndi Safani mlembi, ndi Asaya mnyamata wa mfumu, ndi kuti, Mukani, mundifunsire kwa Yehova, ine ndi otsala m'Israele ndi Yuda, za mau a m'buku lopezekalo; pakuti ukali wa Yehova atitsanulirawu ndi waukulu; popeza makolo athu sanasunge mau a Yehova kuchita monga mwa zonse zolembedwa m'bukumu. Namuka Hilikiya ndi iwo aja adawauza mfumu kwa Hulida mneneri wamkazi, mkazi wa Salumu mwana wa Tokati, mwana wa Hasira wosunga zovala, amene anakhala m'Yerusalemu m'dera lachiwiri, nanena naye mwakuti. Ndipo iye ananena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Muuze munthuyo anakutumizani kwa ine, Atero Yehova, Taonani, ndifikitsira malo ano ndi anthu okhala m'mwemo choipa, ndicho matemberero onse olembedwa m'buku adaliwerenga pamaso pa mfumu ya Yuda; chifukwa anandisiya Ine, nafukizira milungu ina, kuti autse mkwiyo wanga ndi ntchito zonse za manja ao; chifukwa chake ukali wanga utsanulidwa pamalo pano wosazimika. Koma kwa mfumu ya Yuda amene anakutumizani kufunsira kwa Yehova, muzitero kwa iye, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Kunena za mau udawamva, popeza mtima wako unali woolowa, ndipo wadzichepetsa pamaso pa Mulungu, pakumva mau ake otsutsana nao malo ano, ndi okhala m'mwemo, ndi kudzichepetsa pamaso panga, ndi kung'amba zovala zako, ndi kulira pamaso panga; Inenso ndakumvera, ati Yehova. Taona, ndidzakusonkhanitsa kumakolo ako, nudzaikidwa kumanda kwako mumtendere, ndi maso ako sadzapenya zoipa zonse ndidzafikitsira malo ano ndi okhala m'mwemo. Ndipo anambwezera mfumu mau. Pamenepo mfumu inatumiza anthu, nisonkhanitsa akuluakulu onse a Yuda ndi Yerusalemu. Nikwera mfumu kunyumba ya Yehova ndi amuna onse a m'Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu, ndi ansembe ndi Alevi, ndi anthu onse akulu ndi ang'ono; nawerenga iye m'makutu mwao mau onse a buku la chipangano adalipeza m'nyumba ya Yehova. Ndipo mfumu inaimirira pokhala pake, nichita pangano pamaso pa Yehova, kuti adzayenda chotsata Yehova, ndi kusunga malamulo ake, ndi mboni zake, ndi malemba ake, ndi mtima wake wonse, ndi moyo wake wonse, kuchita mau a chipangano olembedwa m'bukumu. Naimiritsapo onse okhala m'Yerusalemu ndi m'Benjamini. Ndipo okhala m'Yerusalemu anachita monga mwa chipangano cha Mulungu, Mulungu wa makolo ao. Yosiya nachotsa zonyansa zonse m'maiko onse okhala a ana a Israele, natumikiritsa onse opezeka m'Israele, inde kutumikira Yehova Mulungu wao. Masiku ake onse iwo sanapatuke kusamtsata Yehova Mulungu wa makolo ao. Pamenepo Yosiya anachitira Yehova Paska m'Yerusalemu, naphera Paska tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi woyamba. Ndipo anaika ansembe pa udikiro wao, nawalimbikitsa achite utumiki wa nyumba ya Yehova. Nati kwa Alevi akuphunzitsa Aisraele onse, ndiwo opatulikira Yehova, Ikani likasa lopatulika m'nyumba imene Solomoni mwana wa Davide mfumu ya Israele anaimanga; silikhalanso katundu pa mapewa anu; tsopano mutumikire Yehova Mulungu wanu, ndi anthu ake Israele. Ndipo mudzikonzere monga mwa nyumba za makolo anu, m'zigawo zanu, monga umo adalembera Davide mfumu ya Israele, ndi umo adalembera Solomoni mwana wake. Ndipo muimirire m'malo opatulika, monga mwa magawidwe a nyumba za makolo za abale anu ana a anthu, akhale nalo onse gawo la nyumba ya makolo ya Alevi. Ndipo muphere Paska, nimudzipatule ndi kukonzera abale anu, kuchita monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose. Ndipo Yosiya anapatsa ana a anthu zoweta, anaankhosa ndi a mbuzi zikhale zonsezo za nsembe za Paska kwa aliyense anali komweko; zinafikira zikwi makumi atatu, ndi ng'ombe zikwi zitatu, ndizo zotapa pa chuma cha mfumu. Ndi akulu ake anapatsa nsembe yaufulu kwa anthu, kwa ansembe, ndi kwa Alevi. Hilikiya ndi Zekariya ndi Yehiyele, atsogoleri a m'nyumba ya Mulungu, anapatsa ansembe zoweta zazing'ono zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi limodzi, ndi ng'ombe mazana atatu, zikhale nsembe za Paska. Konaniyanso, ndi Semaya, ndi Netanele, abale ake, ndi Hasabiya, ndi Yeiyele, ndi Yozabadi, akulu a Alevi, anapatsa Alevi zoweta zazing'ono zikwi zisanu, ndi ng'ombe mazana asanu, zikhale nsembe za Paska. Momwemo anakonzera kutumikiraku, naima ansembe pokhala pao, ndi Alevi m'zigawo zao, monga umo adawauzira mfumu. Pamenepo anaphera Paska; ndi ansembe anawaza mwazi adaulandira m'manja mwa Alevi amene anasenda nsembezo. Ndipo anachotsapo nsembe zopsereza, kuti azipereke kwa ana a anthu monga mwa magawidwe a nyumba za makolo; azipereke kwa Yehova monga mulembedwa m'buku la Mose. Natero momwemo ndi ng'ombezo. Ndipo anaotcha Paska pamoto, monga mwa chiweruzo; koma zopatulikazo anaziphika m'miphika, ndi m'mitsuko, ndi m'ziwaya; nazipereka msanga kwa ana onse a anthu. Ndi pambuyo pake anadzikonzera okha ndi ansembe; popeza ansembe, ana a Aroni, analikupereka nsembe zopsereza ndi mafuta mpaka usiku; chifukwa chake Alevi anadzikonzera okha ndi ansembe ana a Aroni. Ndi oimbira, ana a Asafu, anali pokhala pao, monga adalamulira Davide, ndi Asafu, ndi Hemani, ndi Yedutuni mlauli wa mfumu; ndi olindirira anali pa zipata zonse, analibe kuleka utumiki wao; pakuti abale ao Alevi anawakonzera. Momwemo kutumikira konse kwa Yehova kunakonzeka tsiku lomwelo, kuchita Paska, ndi kupereka nsembe zopsereza pa guwa la nsembe la Yehova, monga analamulira mfumu Yosiya. Ndipo ana a Israele okhalako anachita Paska nthawi yomweyo, ndi chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri. Panalibe Paska wochitika m'Israele wonga ameneyu, kuyambira masiku a Samuele mneneri; panalibenso wina wa mafumu a Israele anachita Paska wotere, ngati ameneyu anachita Yosiya, ndi ansembe, ndi Alevi, ndi Ayuda onse, ndi Aisraele opezekako, ndi okhala m'Yerusalemu. Yosiya atakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri anachita Paska amene. Chitatha ichi chonse, Yosiya atakonza nyumbayi, Neko mfumu ya Aejipito anakwera kuyambana ku Karikemisi ku Yufurate; ndipo Yosiya anamtulukira kuyambana naye. Koma Neko anatuma mithenga kwa iye, ndi kuti, Ndili ndi chiyani ndi inu, mfumu ya Yuda? Sindinafika kuyambana ndi inu lero, koma ndi nyumba imene ndili nayo nkhondo; ndipo Mulungu anati ndifulumire; lekani kuvutana ndi Mulungu amene ali nane, Iye angakuonongeni. Koma Yosiya sanatembenuke nkhope yake kumleka, koma anadzizimbaitsa kuti ayambane naye, osamvera mau a Neko ochokera m'kamwa mwa Mulungu; nadza kuyambana naye m'chigwa cha Megido. Ndipo oponya anayang'anitsa mivi pa mfumu Yosiya, niti mfumu kwa anyamata ake, Ndichotseni ndalasidwa ndithu. Pamenepo anyamata ake anamtulutsa m'galeta, namuika m'galeta wachiwiri anali naye, nabwerera naye ku Yerusalemu; nafa iye naikidwa m'manda a makolo ake. Ayuda onse ndi Yerusalemu nalira Yosiya. Ndipo Yeremiya anamlembera Yosiya nyimbo yomlira; ndi oimbira onse, amuna ndi akazi, amanena za Yosiya nyimbo za maliro zao mpaka lero lino; naziika zikhale lemba m'Israele; taonani, zilembedwa m'Nyimbo za Maliro. Machitidwe ena tsono a Yosiya, ndi ntchito zake zokoma, monga mulembedwa m'chilamulo cha Yehova, ndi zochita iye, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zilembedwa m'buku la mafumu a Israele ndi Yuda. Pamenepo anthu a m'dziko anatenga Yehowahazi mwana wa Yosiya, namlonga ufumu m'Yerusalemu, m'malo mwa atate wake. Yehowahazi anali wa zaka makumi awiri mphambu zitatu polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu miyezi itatu. Ndipo mfumu ya Aejipito anamchotsera ufumu wake m'Yerusalemu, nasonkhetsa dziko matalente zana limodzi a siliva, ndi talente limodzi la golide. Ndi mfumu ya Aejipito anamlonga Eliyakimu mng'ono wake mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu, nasintha dzina lake likhale Yehoyakimu. Koma Neko anatenga Yehowahazi mkulu wake, namuka naye ku Ejipito. Yehoyakimu anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka khumi ndi chimodzi, nachita choipa pamaso pa Yehova Mulungu wake. Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anakwera kuyambana naye, nammanga ndi matangadza kumuka naye ku Babiloni. Nebukadinezara anatenganso ndi zipangizo za nyumba ya Yehova kunka nazo ku Babiloni, naziika m'Kachisi wake ku Babiloni. Machitidwe ena tsono a Yehoyakimu, ndi zonyansa zake anazichita, ndi zija zidapezeka zomtsutsa; taonani, zilembedwa m'buku la mafumu a Israele ndi Yuda; ndi Yehoyakini mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake. Yehoyakini anali wa zaka zisanu ndi zitatu polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu miyezi itatu, ndi masiku khumi; nachita choipa pamaso pa Yehova. Ndipo pofikanso nyengo, mfumu Nebukadinezara anatumiza anthu abwere naye ku Babiloni, pamodzi ndi zipangizo zokoma za nyumba ya Yehova; nalonga Zedekiya mbale wake mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu. Zedekiya anali wa zaka makumi awiri mphambu chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka khumi ndi chimodzi, nachita choipa pamaso pa Yehova Mulungu wake; sanadzichepetse kwa Yeremiya mneneri wakunena zochokera pakamwa pa Yehova. Ndiponso anapandukana naye mfumu Nebukadinezara, amene adamlumbiritsa pa Mulungu; koma anaumitsa khosi lake, nalimbitsa mtima wake kusatembenukira kwa Yehova Mulungu wa Israele. Ndiponso ansembe aakulu onse ndi anthu anachulukitsa zolakwa zao, monga mwa zonyansa zonse za amitundu, nadetsa nyumba ya Yehova, imene anapatula m'Yerusalemu. Ndipo Yehova Mulungu wa makolo ao anatumiza kwa iwo ndi dzanja la mithenga yake, nalawirira mamawa kuituma, chifukwa anamvera chifundo anthu ake, ndi pokhala pake; koma ananyodola mithenga ya Mulungu, napeputsa mau ake, naseka aneneri ake, mpaka ukali wa Yehova unaukira anthu ake, mpaka panalibe cholanditsa. Pakuti Iye anawakweretsera mfumu ya Ababiloni, ndiye anawaphera anyamata ao ndi lupanga, m'nyumba ya malo ao opatulika, osachitira chifundo mnyamata kapena namwali, mkulu kapena nkhalamba; Mulungu anawapereka onse m'dzanja lake. Ndi zipangizo zonse za nyumba ya Mulungu, zazikulu ndi zazing'ono, ndi chuma cha nyumba ya Yehova, ndi chuma cha mfumu, ndi cha akalonga ake, anabwera nazo zonsezi ku Babiloni. Ndipo anatentha nyumba ya Mulungu, nagumula linga la Yerusalemu, natentha nyumba zake zonse zachifumu ndi moto, naononga zipangizo zake zonse zokoma. Ndi iwo amene adapulumuka kulupanga anamuka nao ku Babiloni, nakhala iwo anyamata ake, ndi a ana ake, mpaka mfumu ya Persiya idachita ufumu; kuti akwaniridwe mau a Yehova pakamwa pa Yeremiya, mpaka dziko linakondwera nao masabata ake; masiku onse a kupasuka kwake linasunga Sabata, kukwaniritsa zaka makumi asanu ndi awiri. Chaka choyamba tsono cha Kirusi mfumu ya Persiya, kuti akwaniridwe mau a Yehova pakamwa pa Yeremiya, Yehova anautsa mzimu wa Kirusi mfumu ya Persiya, kuti abukitse mau m'ufumu wake wonse, nawalembenso, ndi kuti, Atero Kirusi mfumu ya Persiya, Yehova Mulungu Wam'mwamba anandipatsa maufumu onse a pa dziko lapansi nandilangiza ndimmangire nyumba m'Yerusalemu, ndiwo ku Yuda. Aliyense mwa inu a anthu ake onse, Yehova Mulungu wake akhale naye, akwereko. Chaka choyamba tsono cha Kirusi mfumu ya ku Persiya, kuti akwaniridwe mau a Yehova m'kamwa mwa Yeremiya, Yehova anautsa mzimu wa Kirusi, kuti abukitse mau m'ufumu wake wonse, nawalembenso, ndi kuti, Atero Kirusi mfumu ya ku Persiya, Yehova Mulungu Wam'mwamba anandipatsa maufumu onse a pa dziko lapansi, nandilangiza ndimmangire nyumba m'Yerusalemu, ndiwo m'Yuda. Aliyense mwa inu a anthu ake onse, Mulungu wake akhale naye, akwere kunka ku Yerusalemu, ndiwo m'Yuda, nakaimange nyumba ya Yehova Mulungu wa Israele; Iye ndiye Mulungu wokhala m'Yerusalemu. Ndipo aliyense wotsala pamalo paliponse agonerapo iye, anthu a kumalo kwake amthandize ndi siliva, ndi golide, ndi zoweta, ndi chuma, pamodzi ndi nsembe yaufulu ya kwa nyumba ya Mulungu ili ku Yerusalemu. Pamenepo ananyamuka akulu a nyumba za makolo a Yuda ndi Benjamini, ndi ansembe, ndi Alevi, ndiwo onse amene Mulungu adawautsira mzimu wao akwere kukamanga nyumba ya Yehova ili ku Yerusalemu. Ndipo onse akuwazinga analimbitsa manja ao ndi zipangizo za siliva, ndi golide, ndi chuma, ndi zoweta, ndi zinthu za mtengo wake, pamodzi ndi nsembe zaufulu. Kirusi mfumu anatulutsanso zipangizo za nyumba ya Yehova, zimene Nebukadinezara adazitulutsa m'Yerusalemu, ndi kuziika m'nyumba ya milungu yake; zomwezi Kirusi mfumu ya ku Persiya anazitulutsa ndi dzanja la Mitiredati wosunga chumayo, naziwerengera Sezibazara kalonga wa Ayuda. Kuwerenga kwake ndiko: mbale zagolide makumi atatu, mbale zasiliva chikwi chimodzi, mipeni makumi awiri mphambu isanu ndi inai; zikho zagolide makumi atatu, zikho zasiliva zina mazana anai ndi khumi, zipangizo zina chikwi chimodzi. Zipangizo zonse zagolide ndi zasiliva ndizo zikwi zisanu ndi mazana anai. Izi zonse Sezibazara anakwera nazo, pokwera andende aja kuchokera ku Babiloni kunka ku Yerusalemu. Ana a deralo, amene anakwera kutuluka m'ndende mwa andende aja Nebukadinezara mfumu ya Babiloni adawatenga ndende kunka nao ku Babiloni, nabwerera kunka ku Yerusalemu ndi Yuda, yense kumudzi wake, ndi awa: ndiwo amene adadza ndi Zerubabele, Yesuwa, Nehemiya, Seraya, Reelaya, Mordekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu, Baana. Kuwerenga kwa amuna a anthu a Israele ndiko: ana a Parosi, zikwi ziwiri ndi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri. Ana a Sefatiya, mazana atatu mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri. Ana a Ara, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi asanu ndi awiri kudza asanu. Ana a Pahatimowabu, a ana a Yesuwa ndi Yowabu, zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi atatu kudza khumi ndi awiri. Ana a Elamu, chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi asanu ndi anai. Ana a Zatu, mazana asanu ndi anai mphambu makumi anai kudza asanu. Ana a Zakai, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi. Ana a Bani, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi anai kudza awiri. Ana a Bebai, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi awiri kudza awiri. Ana a Azigadi, chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi awiri ndi awiri. Ana a Adonikamu, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi mmodzi. Ana a Bigivai, zikwi ziwiri mphambu makumi asanu kudza asanu ndi mmodzi. Ana a Adini, mazana anai mphambu makumi asanu kudza anai. Ana a Atere, a Hezekiya, makumi asanu ndi anai mphambu asanu ndi atatu. Ana a Bezai, mazana atatu mphambu makumi awiri kudza atatu. Ana a Yora, zana limodzi mphambu khumi ndi awiri. Ana a Hasumu, mazana awiri mphambu makumi awiri kudza atatu. Ana a Gibara, makumi asanu ndi anai mphambu asanu. Ana a Betelehemu zana limodzi mphambu makumi awiri kudza atatu. Anthu a ku Netofa, makumi asanu mphambu asanu ndi mmodzi. Anthu a ku Anatoti, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu. Ana a Azimaveti, makumi anai mphambu awiri. Ana a Kiriyati-Arimu, Kefira, ndi Beeroti, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi anai kudza atatu. Ana a Rama ndi Geba, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi awiri kudza mmodzi. Anthu a Mikimasi, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza awiri. Anthu a ku Betele ndi Ai, mazana awiri mphambu makumi awiri kudza atatu. Ana a Nebo, makumi asanu mphambu awiri. Ana a Magabisi, zana limodzi mphambu makumi asanu kudza asanu ndi mmodzi. Ana a Elamu wina, chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi asanu ndi anai. Ana a Harimu, mazana atatu mphambu makumi awiri. Ana a Lodi, Hadidi, ndi Ono, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi awiri kudza asanu. Ana a Yeriko, mazana atatu mphambu makumi anai kudza asanu. Ana a Senaa, zikwi zitatu mphambu mazana asanu ndi limodzi kudza makumi atatu. Ansembe: ana a Yedaya, a nyumba ya Yesuwa, mazana asanu ndi anai mphambu makumi asanu ndi awiri kudza atatu. Ana a Imeri, chikwi chimodzi mphambu makumi asanu kudza awiri. Ana a Pasuri, chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi anai ndi asanu ndi awiri. Ana a Harimu, chikwi chimodzi mphambu khumi limodzi kudza asanu ndi awiri. Alevi: ana a Yesuwa, ndi Kadimiyele, ndiwo a ana a Hodaviya, makumi asanu ndi awiri mphambu anai. Oimba: ana a Asafu, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu. Ana a odikira: ana a Salumu, ana a Atere, ana a Talimoni, ana a Akubu, ana a Hatita, ana a Sobai, onse pamodzi ndiwo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza asanu ndi anai. Anetini: ana a Ziha, ana a Hasufa, ana a Tabaoti, ana a Kerosi, ana a Siyaha, ana a Padoni, ana a Lebana, ana a Hagaba, ana a Akubu, ana a Hagabu, ana a Salimai, ana a Hanani, ana a Gidele, ana a Gahara, ana a Reaya, ana a Rezini, ana a Nekoda, ana a Gazamu, ana a Uza, ana a Paseya, ana a Besai, ana a Asina, ana a Meunimu, ana a Nefisimu, ana a Bakibuki, ana a Hakufa, ana a Harihuri, ana a Baziluti, ana a Mehida, ana a Harisa, ana a Barikosi, ana a Sisera, ana a Tema, ana a Neziya, ana a Hatifa. Ana a akapolo a Solomoni: ana a Sotai, ana a Sofereti, ana a Peruda, ana a Yaala, ana a Darikoni, ana a Gidele, ana a Sefatiya, ana a Hatili, ana a Pokereti-Hazebaimu, ana a Ami. Anetini onse, ndi ana a akapolo a Solomoni, ndiwo mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai kudza awiri. Ndipo okwera kuchokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adani, Imeri, ndi awa, koma sanakhoze kutchula nyumba za makolo ao ndi mbumba zao ngati ali Aisraele: ana a Delaya, ana a Tobiya, ana a Nekoda, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu kudza awiri. Ndi ana a ansembe: ana a Habaya, ana a Hakozi, ana a Barizilai, amene anadzitengera mkazi wa ana akazi a Barizilai Mgiliyadi, natchedwa dzina lao. Awa anafunafuna maina ao m'buku la iwo owerengedwa mwa chibadwidwe chao, koma osawapeza; potero anachotsedwa ku ntchito ya nsembe monga odetsedwa. Ndipo kazembe anawauza kuti asadyeko zopatulika kwambiri, mpaka adzabuka wansembe wokhala ndi Urimu ndi Tumimu. Msonkhano wonse pamodzi ndiwo wa zikwi makumi anai ndi awiri mphambu mazana atatu kudza makumi asanu ndi limodzi, osawerenga akapolo ao aamuna ndi aakazi, ndiwo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana atatu ndi makumi atatu kudza asanu ndi awiri; ndipo anakhala nao aamuna ndi aakazi oimbira mazana awiri. Akavalo ao ndiwo mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu kudza asanu ndi mmodzi; nyuru zao mazana awiri mphambu makumi anai kudza zisanu; ngamira zao mazana anai mphambu makumi atatu kudza asanu; abulu zikwi zisanu ndi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi awiri. Ndipo akulu ena a nyumba za makolo, pofika kunyumba ya Yehova ili ku Yerusalemu, anapereka chaufulu kwa nyumba ya Mulungu chakuiimika pakuzika pake. Monga momwe anakhoza anapereka kuchuma cha ntchitoyi madariki agolide zikwi zisanu ndi chimodzi, miyeso ya mina ya siliva zikwi zisanu, ndi malaya a ansembe zana limodzi. Ndipo ansembe, ndi Alevi, ndi anthu ena, ndi oimbira, ndi odikira, ndi Anetini, anakhala m'midzi mwao, ndi Aisraele onse m'midzi mwao. Utakhala tsono mwezi wachisanu ndi chiwiri, ana a Israele ali m'midzimo, anthuwo anasonkhana ngati munthu mmodzi ku Yerusalemu. Nanyamuka Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ake ansembe, ndi Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi abale ake, namanga guwa la nsembe la Mulungu wa Israele, kuperekapo nsembe zopsereza, monga mulembedwa m'chilamulo cha Mose munthu wa Mulungu. Ndipo anakhazika guwa la nsembe patsinde pake chifukwa cha kuopa iwo anthu a m'maikomo; nakwezera Yehova nsembe zopsereza pamenepo, nsembe zopsereza zam'mawa ndi zamadzulo. Nachita chikondwerero cha Misasa monga kwalembedwa, napereka nsembe yopsereza tsiku ndi tsiku mawerengedwe ake, monga mwa lamulo lake la tsiku lake pa tsiku lake; atatero anaperekanso nsembe yopsereza yosalekeza, ndi za pokhala mwezi, ndi za nyengo zoikika zonse za Yehova zopatulika, ndi za munthu yense wopereka nsembe yaufulu kwa Yehova mwaufulu. Chiyambire tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri anapereka nsembe zopsereza kwa Yehova; koma sanamange maziko a Kachisi wa Yehova. Anaperekanso ndalama kwa amisiri a miyala, ndi a mitengo; ndi chakudya, ndi chakumwa, ndi mafuta, kwa a ku Sidoni, ndi a ku Tiro, kuti atenge mikungudza ku Lebanoni, kufika nayo ku nyanja ku Yopa, monga adawalola Kirusi mfumu ya Persiya. Chaka chachiwiri tsono chakufika iwo kunyumba ya Mulungu ku Yerusalemu, mwezi wachiwiri, Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ao otsala, ansembe ndi Alevi, ndi onse ochokera kundende kudza ku Yerusalemu, anayamba, naika Alevi a zaka makumi awiri ndi mphambu, ayang'anire ntchito ya nyumba ya Yehova. Pamenepo anaimirira pamodzi Yesuwa ndi ana ake ndi abale ake, Kadimiyele ndi ana ake, ana a Yuda, kuyang'anira ogwira ntchito m'nyumba ya Yehova, ana a Henadadi ndi ana ao ndi abale ao Alevi. Ndipo pomanga maziko a Kachisi wa Yehova, amisiriwo anaimiritsa ansembe ovala zovala zao ndi mphalasa, ndi Alevi ana a Asafu ndi nsanje, kuti alemekeze Yehova, monga umo anaikiratu Davide mfumu ya Israele. Ndipo anathirirana mang'ombe, kulemekeza ndi kuyamika Yehova, ndi kuti, Pakuti ndiye wabwino, pakuti chifundo chake nchosalekeza pa Israele. Nafuula anthu onse ndi chimfuu chachikulu, pomlemekeza Yehova; popeza adamanga maziko a nyumba ya Yehova. Koma ansembe ambiri, ndi Alevi, ndi akulu a nyumba za makolo, okalamba amene adaona nyumba yoyamba ija, pomanga maziko a nyumba iyi pamaso pao, analira ndi mau akulu; koma ambiri anafuulitsa mokondwera. Potero anthu sanazindikire phokoso la kufuula mokondwera kulisiyanitsa ndi phokoso la kulira kwa anthu; pakuti anthu anafuulitsa kwakukulu, ndi phokoso lake lidamveka kutali. Atamva tsono adani a Yuda ndi Benjamini kuti ana aja a ndende analikumangira Yehova Mulungu wa Israele Kachisi, anayandikira kwa Zerubabele, ndi kwa akulu a nyumba za makolo, nanena nao, Timange pamodzi nanu; pakuti timfuna Mulungu wanu monga inu, ndipo timamphera nsembe chiyambire masiku a Esarahadoni mfumu ya Asiriya, amene anatikweretsa kuno. Koma Zerubabele, ndi Yesuwa, ndi akulu otsala a nyumba za makolo a Israele, anati kwa iwo, Sikuyenera ndi inu ndi ife kumangira Mulungu wathu nyumba, koma ife tokha pamodzi tidzamangira Yehova Mulungu wa Israele, monga mfumu Kirusi mfumu ya Persiya watilamulira. Pamenepo anthu a m'dziko anafoketsa manja a anthu Ayuda, nawavuta pomanga, nalembera opangira atsutsane nao, nafafanize uphungu wao, masiku onse a Kirusi mfumu ya Persiya, mpaka ufumu wa Dariusi mfumu ya Persiya. Ndipo pokhala mfumu Ahasuwero, poyambira ufumu wake, analembera chowaneneza okhala m'Yuda ndi m'Yerusalemu. Ndipo masiku a Arita-kisereksesi Bisilamu, Mitiredati, Tabeele, ndi anzao otsala, analembera kwa Arita-kisereksesi mfumu ya Persiya; ndi chilembedwe chake cha kalatayo anamlemba m'Chiaramu, namsanduliza m'Chiaramu. Rehumu chiwinda cha malamulo, ndi Simisai mlembi, analemba kalata kwa mfumu Arita-kisereksesi, wakutsutsana naye Yerusalemu motere: nalembera Rehumu chiwinda cha malamulo, ndi Simisai mlembi, ndi anzake otsala; Adinai, ndi Afarisatikai, Ataripilai, Afarisai, Aereke, Ababiloni, Asusani, Adehai, Aelamu, ndi amitundu otsala amene, Osinapara wamkulu ndi womveka adawatenga mikoli, nawakhalitsa m'mudzi wa Samariya, ndi m'dziko lotsala tsidya lino la mtsinje wa Yufurate. Zolembedwa m'kalatayo ndizo: Kwa Arita-kisereksesi mfumu, ife akapolo anu, anthu a tsidya lino la mtsinjewo, tikupatsani moni. Adziwe mfumu kuti, Ayuda adakwerawo ochokera kwanu atifikira ife ku Yerusalemu, alikumanga mudzi uja wopanduka ndi woipa, alikutsiriza malinga ake, nalumikiza maziko ake. Adziwe tsono mfumu, kuti akamanga mudzi uwu ndi kutsiriza malinga ake, sadzapereka msonkho, kapena thangata, kapena msonkho wa m'njira; ndipo potsiriza pake kudzasowetsa mafumu. Popeza tsono timadya mchere wa m'nyumba ya mfumu, sitiyenera kungopenyerera mpepulo wa pa mfumu; chifukwa chake tatumiza ndi kudziwitsa mfumu, kuti afunefune m'buku la chikumbutso la makolo anu; momwemo mudzapeza m'buku la chikumbutso, ndi kudziwa kuti mudzi uwu ndi mudzi wopanduka, ndi wosowetsa mafumu, ndi maiko; ndi kuti amadziyendera m'menemo kuyambira kale lomwe; ndicho chifukwa chakuti anapasula mudzi uwu. Tili kudziwitsa mfumu kuti ukamangidwa mudziwu, nakatsirizidwa malinga ake, simudzakhala nalo gawo tsidya lino la mtsinjewo. Mfumu nibweza mau kwa Rehumu chiwinda cha malamulo, ndi kwa Simisai mlembi, ndi kwa anzao otsala okhala m'Samariya, ndi otsala tsidya lino la mtsinjewo, Mtendere, ndi nthawi yakuti. Kalatayo mwatitumizira anandiwerengera momveka. Ndipo ndinalamulira anthu, nafunafuna, napeza kuti mudzi uwu unaukira mafumu kuyambira kale lomwe, ndi kuti akachitamo mpanduko ndi kudziyendera. Panalinso mafumu amphamvu m'Yerusalemu amene anachita ufumu tsidya lija lonse la mtsinje, ndipo anthu anawapatsa msonkho, thangata, ndi msonkho wa m'njira. Mulamulire tsono kuti anthu awa aleke, ndi kuti asamange mudzi uwu, mpaka ndidzalamulira ndine. Chenjerani mungadodomepo, chidzakuliranji chisauko cha kusowetsa mafumu? Pamenepo atawerenga malemba a kalata wa mfumu Arita-kisereksesi kwa Rehumu, ndi Simisai mlembi, ndi anzao, anafulumira kupita ku Yerusalemu kwa Ayuda, nawaletsa ndi dzanja lamphamvu. Momwemo inalekeka ntchito ya nyumba ya Mulungu yokhala ku Yerusalemu; nilekeka mpaka chaka chachiwiri cha ufumu wa Dariusi mfumu ya Persiya. Ndipo aneneri, Hagai mneneriyo, ndi Zekariya mwana wa Ido, ananenera kwa Ayuda okhala m'Yuda ndi m'Yerusalemu; m'dzina la Mulungu wa Israele ananenera kwa iwo. Pamenepo Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki, ananyamuka, nayamba kumanga nyumba ya Mulungu ili ku Yerusalemu, anali pamodzi nao aneneri a Mulungu akuwathandiza. Nthawi yomweyi anawadzera Tatenai kazembe tsidya lino la mtsinjewo, ndi Setari-Bozenai, ndi anzao, nanena nao motere, Anakulamulirani inu ndani kumanga nyumba iyi, ndi kutsiriza khoma ili? Nanena naonso motere, Maina ao a anthu omanga chimangidwe ichi ndiwo ayani? Koma diso la Mulungu wao linali pa akulu a Ayuda, ndipo sanawaletse mpaka mlandu unamdzera Dariusi, nabweza mau a mlanduwo m'kalata. Zolembedwa m'kalata amene Tatenai kazembe wa tsidya lino la mtsinjewo, ndi Setari-Bozenai, ndi anzake Afarisikai, okhala tsidya lino la mtsinje, anatumiza kwa Dariusi mfumu, anatumiza kalata kwa iyeyo m'menemo munalembedwa motere, kwa Dariusi mfumu, mtendere wonse. Adziwe mfumu kuti ife tinamuka kudziko la Yuda, kunyumba ya Mulungu wamkulu, yomangidwa ndi miyala yaikulu, niikidwa mitengo pamakoma, nichitika mofulumira ntchitoyi, nikula m'dzanja mwao. Pamenepo tinafunsa akulu aja ndi kutere nao, Anakulamulirani ndani kumanga nyumba iyi, ndi kutsiriza khoma ili? Tinawafunsanso maina ao, kukudziwitsani, kuti tilembere maina a anthu akuwatsogolera. Natiyankha mau motere, ndi kuti, Ife ndife akapolo a Mulungu wa Kumwamba ndi dziko lapansi, tilikumanga nyumba imene idamangika zapita zaka zambiri; inaimanga ndi kuitsiriza mfumu yaikulu ya Israele. Koma makolo athuwo atautsa mkwiyo wa Mulungu wa Kumwamba, Iye anawapereka m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni Mkaldeya, amene anaononga nyumba yino, natenga anthu ndende kunka nao ku Babiloni. Koma chaka choyamba cha Kirusi mfumu ya Babiloni, Kirusi mfumuyo analamulira kuti azimanga nyumba iyi ya Mulungu. Ndiponso zipangizo za golide ndi siliva za nyumba ya Mulungu, anazitulutsa Nebukadinezara m'Kachisi anali ku Yerusalemu, ndi kubwera nazo ku Kachisi wa ku Babiloni, izizo Kirusi mfumu anazitulutsa m'Kachisi wa ku Babiloni, nazipereka kwa munthu dzina lake Sezibazara, amene anamuika akhale kazembe; nati naye, Tenga zipangizo izi, kaziike m'Kachisi ali m'Yerusalemu, nimangidwe nyumba ya Mulungu pambuto pake. Pamenepo anadza Sezibazara yemweyo namanga maziko a nyumba ya Mulungu ili m'Yerusalemu; ndipo kuyambira pomwepo kufikira tsopano ilinkumangidwa, koma siinatsirizike. Ndipo tsono chikakomera mfumu, munthu asanthule m'nyumba ya chuma cha mfumu ili komwe ku Babiloni, ngati nkuterodi, kuti Kirusi mfumu analamulira kuti azimanga nyumba iyi ya Mulungu ku Yerusalemu; ndipo mfumu ititumizire mau omkomera pa chinthuchi. Pamenepo analamulira Dariusi mfumu, ndipo anthu anafunafuna m'nyumba ya mabuku mosungira chuma m'Babiloni. Napeza ku Ekibatana m'nyumba ya mfumu m'dera la Mediya, mpukutu, ndi m'menemo munalembedwa motere, chikhale chikumbutso: Chaka choyamba cha Kirusi mfumu, analamulira Kirusi mfumuyo, Kunena za nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu, imangidwe nyumbayi pamalo pophera nsembe, namangidwe kolimba maziko ake, msinkhu wake mikono makumi asanu ndi limodzi, kupingasa kwake mikono makumi asanu ndi limodzi; ndi mipambo itatu ya miyala yaikulu, ndi mpambo wa mitengo yatsopano; nalipidwe ndalama zochokera kunyumba ya mfumu. Ndi zipangizo za golide ndi siliva za nyumba ya Mulungu, zimene anazitulutsa Nebukadinezara m'Kachisi ali ku Yerusalemu, nazitenga kunka nazo ku Babiloni, azibwezere, nabwere nazo ku Kachisi ali ku Yerusalemu, chilichonse ku malo ake; naziike m'nyumba ya Mulungu. Tsono iwe, Tatenai, kazembe wa tsidya lija la mtsinjewo, Setari-Bozenai, ndi anzanu Afarisikai, okhala tsidya lija la mtsinje, muzikhala kutali; lekani ntchito iyi ya Mulungu, osaivuta; kazembe wa Ayuda ndi akulu a Ayuda amange nyumba iyi ya Mulungu pambuto pake. Ndilamuliranso za ichi muzichitira akulu awa a Ayuda, kuti amange nyumba iyi ya Mulungu, ndiko kuti mutengeko chuma cha mfumu, ndicho msonkho wa tsidya la mtsinje, nimupereke zolipira kwa anthu awa msanga, angawachedwetse. Ndipo zosowa zao, anaang'ombe, ndi nkhosa zamphongo, ndi anaankhosa, zikhale nsembe zopsereza za Mulungu wa Kumwamba; tirigu, mchere, vinyo, mafuta, monga umo adzanena ansembe ali ku Yerusalemu, ziperekedwe kwa iwo tsiku ndi tsiku, zisasoweke; kuti apereke nsembe zonunkhira bwino kwa Mulungu wa Kumwamba, napempherere moyo wa mfumu ndi wa ana ake. Ndalamuliranso kuti aliyense adzasintha mau awa, usololedwe mtanda kunyumba kwake, namkweze, nampachike pomwepo; niyesedwa dzala nyumba yake chifukwa cha ichi; ndipo Mulungu wokhalitsa dzina lake komweko agwetse mafumu onse ndi mitundu yonse ya anthu, akutulutsa dzanja lao kusintha mau awa, kuononga nyumba ya Mulungu ili ku Yerusalemu. Ine Dariusi ndalamulira, chichitike msanga. Pamenepo Tatenai kazembe wa tsidya lino la mtsinjewo, Setari-Bozenai, ndi anzao, popeza mfumu Dariusi adatumiza mau, anachita momwemo chofulumira. Ndipo akulu a Ayuda anamanga opanda chosoweka, mwa kunenera kwa mneneri Hagai, ndi Zekariya mwana wa Ido. Naimanga, naitsiriza, monga mwa lamulo la Mulungu wa Israele, ndi monga mwa lamulo la Kirusi, ndi Dariusi, ndi Arita-kisereksesi mfumu ya Persiya. Nitsirizidwa nyumba iyi tsiku lachitatu la mwezi wa Adara, ndicho chaka chachisanu ndi chimodzi cha ufumu wa Dariusi mfumu. Ndipo ana a Israele, ansembe ndi Alevi, ndi ana otsala a ndende, anapereka nyumba iyi ya Mulungu mokondwera. Ndipo popatulira nyumba iyi ya Mulungu anapereka ng'ombe zana limodzi, nkhosa zamphongo mazana awiri, anaankhosa mazana anai, ndi za nsembe yazolakwa ya Aisraele onse atonde khumi ndi awiri, monga mwa kuwerenga kwake kwa mafuko a Israele. Naika ansembe m'magawo mwao, ndi Alevi m'magawidwe mwao, atumikire Mulungu wokhala ku Yerusalemu, monga mulembedwa m'buku la Mose. Ndipo ana a ndende anachita Paska tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi woyamba. Pakuti ansembe ndi Alevi anadziyeretsa pamodzi, anayera onsewo, naphera Paska chifukwa cha ana onse a ndende, ndi abale ao ansembe, ndi iwo okha. Ndipo ana a Israele obwera kundende, ndi yense wakudzipatulira kuchokera chonyansa cha amitundu, kutsata iwowa, kufuna Yehova Mulungu wa Israele, anadza, nasunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri ndi chimwemwe; pakuti Yehova adawakondweretsa, nawatembenuzira mtima wa mfumu ya Asiriya, kulimbitsa manja ao mu ntchito ya nyumba ya Mulungu, Mulungu wa Israele. Zitatha izi tsono, pokhala mfumu Arita-kisereksesi mfumu ya Persiya, anadza Ezara mwana wa Seraya, mwana wa Azariya, mwana wa Hilikiya, mwana wa Salumu, mwana wa Zadoki, mwana wa Ahitubi, mwana wa Amariya, mwana wa Azariya, mwana wa Meraiyoti, mwana wa Zerahiya, mwana wa Uzi, mwana wa Buki, mwana wa Abisuwa mwana wa Finehasi, mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe wamkulu. Ezara amene anakwera kuchokera ku Babiloni, ndiye mlembi waluntha m'chilamulo cha Mose, chimene Yehova Mulungu wa Israele adachipereka; ndipo mfumu inampatsa chopempha iye chonse, monga linamkhalira dzanja la Yehova Mulungu wake. Nakweranso kunka ku Yerusalemu ena a ana a Israele, ndi ansembe, ndi Alevi, ndi oimbira, ndi odikira, ndi Anetini, chaka chachisanu ndi chiwiri cha Arita-kisereksesi mfumu. Ndipo iye anafika ku Yerusalemu mwezi wachisanu, ndicho chaka chachisanu ndi chiwiri cha mfumu. Pakuti tsiku loyamba la mwezi woyamba, ndilo chiyambi cha ulendo wokwera kuchokera ku Babiloni, ndi tsiku lachimodzi la mwezi wachisanu anafika ku Yerusalemu, monga linamkhalira dzanja lokoma la Mulungu wake. Pakuti Ezara adaikiratu mtima wake kuchifuna chilamulo cha Yehova, ndi kuchichita, ndi kuphunzitsa m'Israele malemba ndi maweruzo. Malemba a kalatayo mfumu Arita-kisereksesi anampatsa Ezara wansembe mlembi, ndiye mlembi wa mau a malamulo a Yehova, ndi malemba ake kwa Israele, ndi awa: Arita-kisereksesi mfumu ya mafumu kwa Ezara wansembe, mlembi wa lamulo la Mulungu wa Kumwamba, mtendere weniweni. Ndilamulira kuti onse a ana a Israele, ndi ansembe ao, ndi Alevi, m'ufumu wanga, ofuna eni ake kumuka ku Yerusalemu, apite nawe. Popeza utumidwa wochokera pamaso pa mfumu ndi aphungu ake asanu ndi awiri, kufunsira za Yuda ndi Yerusalemu monga mwa lamulo la Mulungu wako lili m'dzanja lako, ndi kumuka nazo siliva ndi golide, zimene mfumu ndi aphungu ake, anapereka mwaufulu kwa Mulungu wa Israele, mokhala mwake muli m'Yerusalemu, pamodzi ndi siliva ndi golide zilizonse ukazipeza m'dziko lonse la ku Babiloni, pamodzi ndi chopereka chaufulu cha anthu, ndi cha ansembe, akuperekera mwaufulu nyumba ya Mulungu wao ili ku Yerusalemu; m'mwemo uzifulumira kugula ndi ndalama iyi ng'ombe, nkhosa zamphongo, anaankhosa, pamodzi ndi nsembe zao zaufa, ndi nsembe zao zothira; ndi kuzipereka pa guwa la nsembe la nyumba ya Mulungu wanu yokhala ku Yerusalemu. Ndipo chilichonse chidzakomera iwe ndi abale ako kuchita nazo siliva ndi golide zotsala, ichi muchite monga mwa chifuniro cha Mulungu wanu. Ndipo zipangizozo akupatsa za utumiki wa nyumba ya Mulungu wako, uzipereka pamaso pa Mulungu wa ku Yerusalemu. Ndi zina zotsala zakusowa nyumba ya Mulungu wako, zikayenera uzipereke, uzipereke zochokera kunyumba ya chuma cha mfumu. Ndipo ine Arita-kisereksesi, mfumu ine, ndilamulira osunga chuma onse okhala tsidya lija la mtsinjewo, kuti chilichonse akupemphani Ezara wansembe, mlembi wa lamulo la Mulungu wa Kumwamba, chichitike mofulumira; mpaka matalente a siliva zana limodzi, ndi miyeso ya tirigu zana limodzi, ndi mitsuko ya vinyo zana limodzi, ndi mitsuko ya mafuta zana limodzi, ndi mchere wosauwerenga. Chilichonse Mulungu wa Kumwamba achilamulire chichitikire mwachangu nyumba ya Mulungu wa Kumwamba; pakuti padzakhaliranji mkwiyo pa ufumu wa mfumu ndi ana ake? Tikudziwitsaninso kuti sikudzaloledwa kusonkhetsa aliyense wa ansembe, ndi Alevi, oimbira, odikira, Anetini, kapena antchito a nyumba iyi ya Mulungu msonkho, thangata, kapena msonkho wa panjira. Ndipo iwe Ezara monga mwa nzeru za Mulungu wako ili m'dzanja lako, uike nduna, ndi oweruza milandu, aweruze anthu onse ali tsidya lija la mtsinje, onse akudziwa malamulo a Mulungu wako; ndi wosawadziwayo umphunzitse. Ndipo aliyense wosachita lamulo la Mulungu wako, ndi lamulo la mfumu, mlandu umtsutse msanga, ngakhale kumupha, kapena kumpirikitsa m'dziko, kapena kumlanda chuma chake, kapena kummanga m'kaidi. Wodala Yehova Mulungu wa makolo athu, amene anaika chinthu chotere mu mtima wa mfumu, kukometsera nyumba ya Yehova ili ku Yerusalemu, nandifikitsira chifundo pamaso pa mfumu, ndi aphungu ake, ndi pamaso pa akalonga amphamvu onse a mfumu. Motero ndinalimbika mtima, monga umo dzanja la Yehova Mulungu wanga linakhala pa ine; ndipo ndinasonkhanitsa mwa Israele anthu omveka akwere nane limodzi. Ndipo akulu a nyumba za makolo ndi awa, ndi chibadwidwe cha iwo okwera nane limodzi kuchokera ku Babiloni, pokhala mfumu Arita-kisereksesi, ndi ichi: wa ana a Finehasi, Geresomo; wa ana a Itamara, Daniele; wa ana a Davide, Hatusi. Wa ana a Sekaniya, wa ana a Parosi, Zekariya; ndi pamodzi naye, powawerenga monga mwa chibadwidwe chao, amuna zana limodzi mphambu makumi asanu. Wa ana a Pahatimowabu, Eliehoenai mwana wa Zerahiya; ndi pamodzi naye amuna mazana awiri. Wa ana a Sekaniya, mwana wa Yahaziele; ndi pamodzi naye amuna mazana atatu. Ndi wa ana a Adini, Ebedi mwana wa Yonatani; ndi pamodzi naye amuna makumi asanu. Ndi wa ana a Elamu, Yesaya mwana wa Ataliya; ndi pamodzi naye amuna makumi asanu ndi awiri. Ndi wa ana a Sefatiya, Zebadiya mwana wa Mikaele; ndi pamodzi naye amuna makumi asanu ndi atatu. Wa ana a Yowabu, Obadiya mwana wa Yehiyele; ndi pamodzi naye amuna mazana awiri mphambu khumi kudza asanu ndi atatu. Ndi wa ana a Selomiti, mwana wa Yosofiya; ndi pamodzi naye amuna zana limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi. Ndi wa ana a Bebai, Zekariya mwana wa Bebai; ndi pamodzi naye amuna makumi awiri mphambu asanu ndi atatu. Ndi wa ana a Azigadi, Yohanani mwana wa Hakatani; ndi pamodzi naye amuna zana limodzi mphambu khumi limodzi. Ndi a ana otsiriza a Adonikamu, maina ao ndiwo Elifeleti, Yeiyele, ndi Semaya; ndi pamodzi nao amuna makumi asanu ndi limodzi. Ndi wa ana a Bigivai, Utai ndi Zakuri, ndi pamodzi nao amuna makumi asanu ndi awiri. Ndipo ndinawasonkhanitsa ku mtsinje wopita ku Ahava, ndi komweko tinakhala m'misasa masiku atatu; ndipo ndinapenyerera anthu ndi ansembe, koma sindinapezapo wa ana a Levi. Pamenepo ndinatumiza munthu kuitana Eliyezere, Ariyele, Semaya, ndi Elinatani, ndi Yaribu, ndi Elinatani, ndi Natani, ndi Zekariya, ndi Mesulamu, ndiwo akulu; ndi Yoyaribu ndi Elinatani, ndiwo aphunzitsi. Ndipo ndinawatumiza kwa Ido mkulu, kumalo dzina lake Kasifiya; ndinalonganso m'kamwa mwao mau akunena kwa Ido, ndi kwa abale ake Anetini, pa malo paja Kasifiya, kuti azibwera nao kwa ife otumikira za nyumba ya Mulungu wathu. Ndipo monga munatikhalira dzanja lokoma la Mulungu wathu, anatitengera munthu wanzeru wa ana a Mali, mwana wa Levi, mwana wa Israele; ndi Serebiya, pamodzi ndi ana ake ndi abale ake khumi mphambu asanu ndi atatu; ndi Hasabiya, ndi pamodzi naye Yesaya wa ana a Merari, abale ake ndi ana ao makumi awiri; ndi a Anetini, amene Davide ndi akalonga adapereka atumikire Alevi, Anetini mazana awiri mphambu makumi awiri, onsewo otchulidwa maina. Pamenepo ndinalalikira chosala komweko kumtsinje wa Ahava, kuti tidzichepetse pamaso pa Mulungu wathu, kumfunsa ationetsere njira yolunjika ya kwa ife, ndi ang'ono athu, ndi chuma chathu chonse. Pakuti ndinachita manyazi kupempha kwa mfumu gulu la asilikali, ndi apakavalo, kutithandiza pa adani panjira; popeza tidalankhula ndi mfumu kuti, Dzanja la Mulungu wathu likhalira mokoma onse akumfuna; koma mphamvu yake ndi mkwiyo wake zitsutsana nao onse akumsiya. Momwemo tinasala ndi kupempha ichi kwa Mulungu wathu; nativomereza Iye. Pamenepo ndinapatula akulu a ansembe khumi ndi awiri, ndiwo Serebiya, Hasabiya, ndi abale ao khumi pamodzi nao, ndi kuwayesera siliva, ndi golide, ndi zipangizo, ndizo chopereka cha kwa nyumba ya Mulungu wathu, chimene mfumu, ndi aphungu ake, ndi akalonga ake, ndi Aisraele onse anali apawa, adapereka. Ndipo ndinawayesera m'dzanja mwao matalente a siliva mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu, ndi zipangizo zasiliva matalente zana limodzi, ndi zikho zagolide makumi awiri za madariki chikwi chimodzi, ndi zipangizo ziwiri za mkuwa wabwino wonyezimira wokhumbika ngati golide. Ndipo ndinanena nao, Inu ndinu opatulikira Yehova, ndi zipangizozo nzopatulikira, ndi siliva ndi golide, ndizo chopereka chaufulu cha kwa Yehova Mulungu wa makolo anu. Mukhale maso ndi kuzisunga mpaka muziyesera pamaso pa ansembe aakulu ndi Alevi, ndi akulu a nyumba za makolo a Israele ku Yerusalemu, m'zipinda za nyumba ya Yehova. Potero ansembe ndi Alevi analandira kulemera kwake kwa siliva ndi golide ndi zipangizo, abwere nazo ku Yerusalemu kunyumba ya Mulungu wathu. Pamenepo tinachoka ku mtsinje wa Ahava tsiku lakhumi ndi chiwiri la mwezi woyamba, kunka ku Yerusalemu; ndipo dzanja la Mulungu wathu linakhala pa ife, ndi kutilanditsa m'dzanja la mdani ndi wolalira m'njira. Ndipo tinafika ku Yerusalemu ndi kukhalako masiku atatu. Ndipo pa tsiku lachinai siliva ndi golide ndi zipangizo zinayesedwa m'nyumba ya Mulungu wathu, m'dzanja la Meremoti mwana wa Uriya wansembe, ndi pamodzi naye Eleazara mwana wa Finehasi, ndi pamodzi nao Yozabadi mwana wa Yesuwa, ndi Nowadiya mwana wa Binuyi, Alevi; zonsezi anaziwerenga ndi kuziyesa; ndi kulemera kwake konse kunalembedwa nthawi yomweyo. Otengedwa ndende, atatuluka m'ndende, anapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu wa Israele, ng'ombe khumi ndi ziwiri za Aisraele onse, nkhosa zamphongo makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi imodzi, anaankhosa makumi asanu ndi awiri mphambu asanu ndi awiri, atonde khumi ndi awiri, akhale nsembe yazolakwa; zonsezi ndizo nsembe yopsereza ya kwa Yehova. Ndipo napereka malamulo a mfumu kwa akazembe a mfumu, ndi kwa ziwanga, tsidya lino la mtsinjewo; ndipo iwo anathandiza anthu ndi nyumba ya Mulungu. Zitatha izi tsono anandiyandikira akalonga, ndi kuti, Anthu a Israele, ndi nsembe, ndi Alevi, sanadzilekanitse ndi anthu a maikowa, kunena za zonyansa zao za Akanani, Ahiti, Aperizi, Ayebusi, Aamoni, Amowabu, Aejipito, ndi Aamori. Pakuti anadzitengera okha ndi ana amuna ao ana akazi ao; nisokonezeka mbeu yopatulika ndi mitundu ya maikowa; inde dzanja la akalonga ndi olamulira linayamba kulakwa kumene. Ndipo pakumva mau awa ndinang'amba chovala changa, ndi malaya anga, ndi kumwetula tsitsi la pamutu panga ndi ndevu zanga, ndi kukhala pansi m'kudabwa. Nandisonkhanira aliyense wakunjenjemera pa mau a Mulungu wa Israele, chifukwa cha kulakwa kwa iwo a ndende; ndipo ndinakhala m'kudabwa mpaka nsembe yamadzulo. Ndi pa nsembe yamadzulo ndinanyamuka m'kuzunzika kwanga, chovala changa ndi malaya anga zong'ambika; ndipo ndinagwada ndi maondo anga, ndi kutambasula manja anga kwa Yehova Mulungu wanga; ndipo ndinati, Mulungu wanga, ndigwa nkhope, ndi kuchita manyazi kuweramutsa nkhope yanga kwa inu Mulungu wanga, popeza mphulupulu zathu zachuluka pamtu pathu, ndi kupalamula kwathu kwakula kufikira m'Mwamba. Chiyambire masiku a makolo athu tapalamula kwakukulu mpaka lero lino; ndi chifukwa cha mphulupulu zathu ife, mafumu athu, ndi ansembe athu, tinaperekedwa m'dzanja la mafumu a maikowo, kulupanga kundende, ndi kufunkhidwa, ndi kuchitidwa manyazi pankhope pathu, monga lero lino. Ndipo tsopano, kamphindi, Yehova Mulungu wathu wationetsa chisomo, kutisiyira chipulumutso, ndi kutipatsa chichiri m'malo mwake mopatulika; kuti Mulungu wathu atipenyetse m'maso mwathu, ndi kutitsitsimutsa pang'ono m'ukapolo wathu. Popeza ife ndife akapolo, koma Mulungu wathu sanatisiye m'ukapolo wathu, natifikitsira chifundo pamaso pa mafumu a Persiya, kuti atitsitsimutse kuimika nyumba ya Mulungu wathu, ndi kukonzanso muunda wake, ndi kutipatsa linga m'Yuda ndi m'Yerusalemu. Ndipo tsopano, Mulungu wathu, tidzanenanji pambuyo pa ichi? Pakuti tasiya malamulo anu, amene munalamulira mwa atumiki anu aneneri ndi kuti, Dzikolo mumukako likhale cholowa chanu ndilo dziko lodetsedwa mwa chidetso cha anthu a m'maikomo, mwa zonyansa zao zimene zinalidzaza, kuyambira nsonga ina kufikira nsonga inzake ndi uchisi wao. Chifukwa chake tsono, musamapereka ana anu akazi kwa ana ao amuna, kapena kutengera ana anu amuna ana ao akazi, kapena kufuna mtendere wao ndi kukoma kwao nthawi yonse, kuti mukhale olimba, ndi kudya zokoma za m'dziko, ndi kulisiyira ana anu cholowa cha kunthawi yonse. Ndipo zitatigwera zonsezi chifukwa cha ntchito zathu zoipa ndi kupalamula kwathu kwakukulu; popeza inu Mulungu wathu mwatilanga motichepsera mphulupulu zathu, ndi kutipatsa chipulumutso chotere; kodi tidzabwereza kuphwanya malamulo anu, ndi kukwatana nayo mitundu ya anthu ochita zonyansa izi? Simudzakwiya nafe kodi mpaka mwatitha, ndi kuti pasakhale otsala kapena akupulumuka? Yehova Mulungu wa Israele, Inu ndinu wolungama, popeza tinatsala opulumuka monga lero lino; taonani, tili pamaso panu m'kupalamula kwathu; pakuti palibe wakuima pamaso panu chifukwa cha ichi. Pakupemphera Ezara tsono, ndi kuwulula ndi kulira misozi, ndi kudzigwetsa pansi pakhomo pa nyumba ya Mulungu, udamsonkhanira mwa Israele msonkhano waukulu ndithu wa amuna, ndi akazi, ndi ana; popeza anthu analira kulira kwakukulu. Pamenepo Sekaniya mwana wa Yehiyele, mwana wina wa Elamu, anambwezera Ezara mau, nati, Talakwira Mulungu wathu, tadzitengera akazi achilendo a mitundu ya dzikoli; koma tsopano chimtsalira Israele chiyembekezo kunena za chinthu ichi. Ndipo tsono tipangane ndi Mulungu wathu kuchotsa akazi onse, ndi obadwa mwa iwo, monga mwa uphungu wa mbuye wanga, ndi wa iwo akunjenjemera pa lamulo la Mulungu wathu; ndipo chichitike monga mwa chilamulo. Nyamukani, mlandu ndi wanu; ndipo ife tili nanu; limbikani, chitani. Nanyamuka Ezara, nalumbiritsa akulu a ansembe, ndi Alevi, ndi Aisraele onse, kuti adzachita monga mwa mau awa. Nalumbira iwo. Pamenepo Ezara ananyamuka pakhomo pa nyumba ya Mulungu, nalowa m'chipinda cha Yehohanani mwana wa Eliyasibu, ndipo atafikako sanadye mkate, sanamwe madzi; pakuti anachita maliro chifukwa cha kulakwa kwa iwo otengedwa ndende. Nabukitsa iwo mau mwa Yuda ndi Yerusalemu kwa ana onse otengedwa ndende, kuti azisonkhana ku Yerusalemu; ndi kuti aliyense wosafikako atapita masiku atatu, monga mwa uphungu wa akalonga ndi akulu, chuma chake chonse chidzaonongeka konse, ndipo iye adzachotsedwa kumsonkhano wa iwo otengedwa ndende. Ndipo anasonkhana ku Yerusalemu amuna onse a Yuda ndi Benjamini asanapite masiku atatu, ndiwo mwezi wachisanu ndi chinai, tsiku la makumi awiri a mwezi; nakhala pansi anthu onse m'khwalala pakhomo pa nyumba ya Mulungu, alikunjenjemera chifukwa cha mlandu uwu, ndi chifukwa cha mvulayi. Pamenepo Ezara wansembe ananyamuka, nanena nao, Mwalakwa, mwadzitengera akazi achilendo, kuonjezera kupalamula kwa Israele. Chifukwa chake tsono, wululani kwa Yehova Mulungu wa makolo anu, nimuchite chomkondweretsa; mudzilekanitse ndi mitundu ya anthu a m'dzikomo, ndi kwa akazi achilendo. Ndipo unayankha msonkhano wonse, ndi kunena ndi mau akulu, Monga mwa mau anu tiyenera kuchita. Koma anthu ndiwo ambiri, ndi nyengo yino nja mvula, tilibenso mphamvu yakuima pabwalo, ndi ntchitoyi sindiyo ya tsiku limodzi kapena awiri; pakuti tachulukitsa kulakwa kwathu pa chinthu ichi. Ayang'anire ichi tsono akalonga athu a msonkhano wonse, ndi onse a m'midzi mwathu amene anadzitengera akazi achilendo abwere pa nthawi zoikika, ndi pamodzi nao akulu a mudzi wao uliwonse, ndi oweruza ake, mpaka udzatichokera mkwiyo waukali wa Mulungu wathu chifukwa cha mlandu uwu. Yonatani mwana wa Asahele ndi Yazeya mwana wa Tikiva okha anatsutsana nacho, ndi Mesulamu ndi Sabetai Mlevi anawathandiza. Pamenepo anthu otengedwa ndende anachita chotero. Ndi Ezara wansembe, ndi anthu akulu a nyumba za makolo, monga mwa nyumba za makolo ao, iwo onse otchulidwa maina ao, anasankhidwa, nakhala pansi tsiku loyamba la mwezi wakhumi kufunsa za mlanduwu. Natsiriza nao amuna onse adadzitengera akazi achilendo tsiku loyamba la mwezi woyamba. Ndipo anapeza mwa ana a ansembe odzitengera akazi achilendo, ndiwo a ana a Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ake Maaseiya, ndi Eliyezere, ndi Yaribu, ndi Gedaliya. Ndipo anaimika dzanja lao kuti adzachotsa akazi ao; ndipo popeza adapalamuladi, anapereka nsembe nkhosa yamphongo ya zoweta pa kupalamula kwao. Ndi a ana a Imeri: Hanani ndi Zebadiya. Ndi a ana a Harimu: Maaseiya, ndi Eliya, ndi Semaya, ndi Yehiyele, ndi Uziya. Ndi a ana a Pasuri: Eliyoenai, Maaseiya, Ismaele, Netanele, Yozabadi, ndi Elasa. Ndi a Alevi: Yozabadi, ndi Simei, ndi Kelaya (ndiye Kelita), Petahiya, Yuda, ndi Eliyezere. Ndi a oimbira: Eliyasibu; ndi a odikira: Salumu, ndi Telemu, ndi Uri. Ndi Aisraele a ana a Parosi: Ramiya, ndi Iziya, ndi Matikiya, ndi Miyamini, ndi Eleazara, ndi Malikiya, ndi Benaya. Ndi a ana a Elamu: Mataniya, Zekariya, ndi Yehiyele, ndi Abidi, ndi Yeremoti, ndi Eliya. Ndi a ana a Zatu: Eliyoenai, Eliyasibu, Mataniya, ndi Yeremoti, ndi Zabadi, ndi Aziza. Ndi a ana a Bebai: Yehohanani, Hananiya, Zabai, Atilai. Ndi a ana a Bani: Mesulamu, Maluki, ndi Adaya, Yasubu, ndi Seyala, Yeremoti. Ndi a ana a Pahatimowabu: Adina, ndi Kelali, Benaya, Maaseiya, Mataniya, Bezalele, ndi Binuyi, ndi Manase. Ndi a ana a Harimu: Eliyezere, Isiya, Malikiya, Semaya, Simeoni, Benjamini, Maluki, Semariya. A ana a Hasumu: Matenai, Matata. Zabadi, Elifeleti, Yeremai, Manase, Simei. A ana a Bani: Maadai, Amuramu, ndi Uwele, Benaya, Bedeiya, Keluhu, Vaniya, Meremoti, Eliyasibu, Mataniya, Matenai, ndi Yasu, ndi Bani, ndi Binuyi, Simei, ndi Selemiya, ndi Natani, ndi Adaya, Makinadebai, Sasai, Sarai, Azarele, ndi Selemiya, Semariya, Salumu, Amariya, Yosefe. A ana a Nebo: Yeiyele, Matitiya, Zabadi, Zebina, Yadai, ndi Yowele, Benaya. Awa onse adatenga akazi achilendo, ndi ena a iwowa anali ndi akazi amene adawabalira ana. Mau a Nehemiya mwana wa Hakaliya. Kunali tsono mwezi wa Kisilevi, chaka cha makumi awiri, pokhala ine ku Susa kunyumba ya mfumu, anafika Hanani, mmodzi wa abale anga, iye ndi amuna ena a ku Yuda; ndipo ndinawafunsa za Ayuda adapulumukawo otsala andende, ndi za Yerusalemu. Nanena nane iwo, Otsalawo otsala andende uko kudzikoko akulukutika kwakukulu, nanyozedwa; ndi linga la Yerusalemu lapasuka, ndi zipata zake zatenthedwa ndi moto. Ndipo kunali, pakumva mau awa, ndinakhala pansi ndi kulira misozi, ndi kuchita maliro masiku ena, ndinasalanso, ndi kupemphera pamaso pa Mulungu wa Kumwamba, ndi kuti, Ndikupembedzani Yehova, Mulungu wa Kumwamba, Mulungu wamkulu ndi woopsa, wakusunga pangano ndi chifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ake; mutchere khutu, ndi maso anu atseguke kumvera pemphero la kapolo wanu, ndilipempha pamaso panu tsopano apa msana ndi usiku, kupempherera ana a Israele akapolo anu, ndi kuwulula zoipa za ana a Israele zimene tachimwira nazo Inu; inde tachimwa, ine ndi nyumba ya atate wanga. Tachita mwamphulupulu pa Inu, osasunga malamulo, kapena malemba, kapena maweruzo, amene mudalamulira mtumiki wanu Mose. Mukumbukire mau mudalamulira mtumiki wanu Mose, ndi kuti, Mukalakwa, ndidzakubalalitsani mwa mitundu ya anthu; koma mukabwerera kudza kwa Ine, ndi kusunga malamulo anga, ndi kuwachita, angakhale otayika anu anali ku malekezero a thambo, ndidzawasonkhanitsa kuchokera komweko, ndi kubwera nao kumalo ndinawasankha kukhalitsako dzina langa. Ndipo awa ndi akapolo anu ndi anthu anu, amene munawaombola ndi mphamvu yanu yaikulu, ndi dzanja lanu lolimba. Yehova, mutcherere khutu pemphero la kapolo wanu, ndi pemphero la akapolo anu okondwera nako kuopa dzina lanu; ndipo mupambanitse kapolo wanu lero lino, ndi kumuonetsera chifundo pamaso pa munthu uyu. Koma ndinali ine wothirira mfumu chakumwa chake. Koma kunachitika mwezi wa Nisani, chaka cha makumi awiri cha Arita-kisereksesi mfumu pokhala vinyo pamaso pake, ndinatenga vinyoyo ndi kuipatsa mfumu. Koma sindidakhala wachisoni pamaso pake ndi kale lonse. Ninena nane mfumu, Nkhope yako nja chisoni chifukwa ninji popeza sudwala? Ichi si chinthu china koma chisoni cha mtima. Pamenepo ndinachita mantha akulu. Ndipo ndinati kwa mfumu, Mfumu ikhale ndi moyo kosatha; ilekerenji nkhope yanga kuchita chisoni, popeza pali bwinja kumudzi kuli manda a makolo anga, ndi zipata zake zopsereza ndi moto. Ndipo mfumu inati kwa ine, Ufunanji iwe? Pamenepo ndinapemphera Mulungu wa Kumwamba. Ndipo ndinati kwa mfumu, Chikakomera mfumu, ndi mtima wanu ukakomera kapolo wanu, munditumize ku Yuda kumudzi wa manda a makolo anga, kuti ndiumange. Ninena nane mfumu, ilikukhala pansi pamodzi ndi mkazi wake wamkulu, Ulendo wako ngwa nthawi yanji, udzabweranso liti? Ndipo kudakonda mfumu kunditumiza nditaitchula nthawi. Ndinanenanso kwa mfumu, Chikakomera mfumu, indipatse akalata kwa ziwanga za tsidya lija la mtsinje, andilole ndipitirire mpaka ndifikira ku Yuda; ndi kalata kwa Asafu wosunga misitu ya mfumu, kuti andipatse mitengo ya mitanda ya kuzipata za linga lili ku Kachisi, ndi ya linga la mudzi, ndi ya nyumba imene ndidzalowamo ine. Ndipo mfumu inandipatsa monga mwa dzanja lokoma la Mulungu londikhalira. Ndinafika tsono kwa ziwanga za tsidya lino la mtsinje, ndipo ndinawapatsa akalata a mfumu. Koma mfumu idatumiza apite nane akazembe a nkhondo, ndi apakavalo. Atamva Sanibalati Muhoroni, ndi Tobiya kapoloyo Mwamoni, chidawaipira kwakukulu, kuti wadza munthu kuwafunira ana a Israele chokoma. Motero ndinafika ku Yerusalemu, ndi kukhalako masiku atatu. Ndipo ndinauka usiku, ine ndi amuna owerengeka nane, osauza munthu yense ine choika Mulungu wanga m'mtima mwanga ndichitire Yerusalemu; panalibenso nyama ina nane, koma nyama imene ndinakhalapo. Ndipo ndinatuluka usiku pa Chipata cha ku Chigwa, kunka kuchitsime cha chinjoka, ndi ku Chipata cha Kudzala, ndi kuyang'ana malinga a Yerusalemu adapasukawo, ndi zipata zake zothedwa ndi moto. Ndipo ndinapitirira kunka ku Chipata cha Chitsime, ndi ku Dziwe la Mfumu; koma popita nyama ili pansi panga panaichepera. Ndipo ndinakwera usiku kumtsinje, ndi kuyang'ana lingali; ndinabwerera tsono ndi kulowa pa Chipata cha ku Chigwa, momwemo ndinabwereranso. Koma olamulira sanadziwe uko ndinamuka, kapena chochita ine; sindidauzenso kufikira pamenepo Ayuda, kapena ansembe, kapena aufulu, kapena olamulira, kapena otsala akuchita ntchitoyi. Pamenepo ndinanena nao, Muona choipa m'mene tilimo, kuti Yerusalemu ali bwinja, ndi zipata zake zotentha ndi moto; tiyeni timange linga la Yerusalemu, tisakhalenso chotonzedwa. Ndinawauzanso za dzanja la Mulungu wanga londikhalira mokoma, ndiponso za mau anandiuza mfumu. Nati iwo, Tinyamuke, timange. Chotero anandilimbitsira manja mokoma. Koma Sanibalati Muhoroni, ndi Tobiya kapolo Mwamoniyo, ndi Gesemu Mwarabu, anamva natiseka pwepwete, natipeputsa, nati, Chiyani ichi muchichita? Mulikupandukira mfumu kodi? Koma ndinawabwezera mau, ndi kunena nao, Mulungu Wam'mwamba, Iye ndiye adzatilemeza; chifukwa chake ife akapolo ake tidzanyamuka ndi kumanga; koma inu mulibe gawo, kapena ulamuliro, kapena chikumbukiro, m'Yerusalemu. Pamenepo Eliyasibu mkulu wa ansembe ananyamuka pamodzi ndi abale ake ansembe, namanga chipata chankhosa; anachipatula, naika zitseko zake, inde anachipatula mpaka Nsanja ya Zana, mpaka nsanja ya Hananele. Ndi pambali pake anamanga amuna a ku Yeriko. Ndi pambali pao anamanga Zakuri mwana wa Imuri. Ndi chipata chansomba anachimanga ana a Hasena; anamanga mitanda yake, ndi kuika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipingiridzo yake. Ndi pambali pao anakonza Meremoti mwana wa Uriya, mwana wa Hakozi. Ndi pambali pao anakonza Mesulamu mwana wa Berekiya, mwana wa Mesezabele. Ndi pambali pao anakonza Zadoki mwana wa Baana. Ndi pambali pao anakonza Atekowa; koma omveka ao sanapereke makosi ao kuntchito ya Mbuye wao. Ndi chipata chakale anachikonza Yoyada mwana wa Paseya; ndi Mesulamu mwana wa Besodeiya anamanga mitanda yake, ndi kuika zitseko zake, ndi zokowera zake, ndi mipingiridzo yake. Ndi pambali pao anakonza Melatiya Mgibeoni, ndi Yadoni Mmeronoti, ndi amuna a ku Gibiyoni, ndi a ku Mizipa, wa ulamuliro wa chiwanga tsidya lino la mtsinje. Pambali pake anakonza Uziyele mwana wa Haraya, wa iwo osula golide. Ndi padzanja pake anakonza Hananiya, wa iwo osanganiza zonunkhira; nalimbikitsa Yerusalemu mpaka linga lachitando. Ndi pambali pao anakonza Refaya mwana wa Huri, ndiye mkulu wa dera lina la dziko la Yerusalemu. Ndi pambali pao anakonza Yedaya mwana wa Harumafa, pandunji pa nyumba yake. Ndi pambali pake anakonza Hatusi mwana wa Hasabineya. Malikiya mwana wa Harimu, ndi Hasubu mwana wa Pahatimowabu, anakonza gawo lina, ndi Nsanja ya Ng'anjo. Ndi pambali pake anakonza Salumu mwana wa Halohesi, mkulu wa dera lina la dziko la Yerusalemu, iye ndi ana ake akazi. Chipata cha ku Chigwa anachikonza Hanuni; ndi okhala m'Zanowa anachimanga, naika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipiringidzo yake; ndiponso mikono chikwi chimodzi cha lingalo mpaka ku Chipata cha Kudzala. Ndi Chipata cha Kudzala anachikonza Malikiya mwana wa Rekabu, mkulu wa dziko la Betehakeremu; anachimanga, naika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipiringidzo yake. Ndi chipata cha kukasupe anachikonza Salumu mwana wa Kolihoze mkulu wa dziko la Mizipa anachimanga, nachikomaniza pamwamba pake, naika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipiringidzo yake; ndiponso linga la dziwe la Sela pa munda wa mfumu, ndi kufikira kumakwerero otsikira kumudzi wa Davide. Potsatizana naye anakonza Nehemiya mwana wa Azibuki, mkulu wa dera lake lina la dziko la Betezuri, mpaka malo a pandunji pa manda a Davide, ndi ku dziwe adalikumba, ndi kunyumba ya amphamvu aja. Potsatizana naye anakonza Alevi, Rehumu mwana wa Bani. Pambali pake anakonza Hasabiya mkulu wa dera lina la dziko la Keila, kukonzera dziko lake. Potsatizana naye anakonza abale ao, Bavai mwana wa Henadadi, mkulu wa dera lina la dziko la Keila. Ndi pa mbali pake Ezere mwana wa Yesuwa, mkulu wa Mizipa, anakonza gawo lina, pandunji pokwerera kunyumba yosungamo zida za nkhondo, popindirira linga. Potsatizana naye Baruki mwana wa Zabai anafulumira kukonza gawo lina kuyambira popindirira mpaka kukhomo la nyumba ya Eliyasibu mkulu wa ansembe. Potsatizana naye Meremoti mwana wa Uriya mwana wa Hakozi anakonza gawo lina, kuyambira kukhomo la nyumba ya Eliyasibu kufikira malekezero ake a nyumba ya Eliyasibu. Ndi potsatizana naye anakonza ansembe okhala kuchidikha. Potsatizana nao anakonza Benjamini ndi Hasubu pandunji pa nyumba pao. Potsatizana nao anakonza Azariya mwana wa Maaseiya mwana wa Ananiya pafupi pa nyumba yake. Potsatizana naye Binuyi mwana wa Henadadi anakonza gawo lina, kuyambira kunyumba ya Azariya kufikira popindirira kufikira kungodya. Palali mwana wa Uzai anakonza pandunji popindirira, ndi nsanja yosomphoka pa nyumba ya mfumu ya kumtunda, imene ili kubwalo la kaidi. Potsatizana naye anakonza Pedaya mwana wa Parosi. Koma Anetini okhala m'Ofele anakonza kufikira kumalo a pandunji pa Chipata cha Madzi kum'mawa, ndi nsanja yosomphokayo. Potsatizana nao Atekowa anakonza gawo lina, pandunji pa nsanja yaikulu yosomphoka ndi kulinga la Ofele. Kumtunda kwa chipata cha akavalo anakonza ansembe, yense pandunji pa nyumba yake. Potsatizana nao anakonza Zadoki mwana wa Imeri pandunji pa nyumba yake. Ndi potsatizana naye anakonza Semaya mwana wa Sekaniya, wosunga chipata cha kum'mawa. Potsatizana naye Hananiya mwana wa Selemiya, ndi Hanuni mwana wachisanu ndi chimodzi wa Zalafi, anakonza gawo lina. Potsatizana naye anakonza Mesulamu mwana wa Berekiya pandunji pa chipinda chake. Potsatizana naye anakonza Malikiya wina wa osula golide kufikira kunyumba ya Anetini, ndi ya ochita malonda, pandunji pa chipata cha Hamifikadi, ndi kuchipinda chosanja cha kungodya. Ndi pakati pa chipinda chosanja cha kungodya ndi chipata chankhosa anakonza osula golide ndi ochita malonda. Ndipo kunali, atamva Sanibalati kuti tinalikumanga lingali, kudamuipira, nakwiya kwakukulu, naseka Ayuda pwepwete. Nanena iye pamaso pa abale ake ndi ankhondo a ku Samariya, nati, Alikuchitanji Ayuda ofookawa? Adzimangire linga kodi? Adzapereka nsembe kodi? Adzatsiriza tsiku limodzi kodi? Adzakometsanso miyala ya ku miunda yotenthedwa? Ndipo Tobiya Mwamoni anali naye, nati, Chinkana ichi achimanga, ikakwerako nkhandwe, idzagamula linga lao lamiyala. Imvani, Mulungu wathu, popeza tanyozeka ife; muwabwezere chitonzo chao pamtu pao, ndi kuwapereka akhale chofunkhidwa m'dziko la ndende; ndipo musakwirira mphulupulu yao, ndi kulakwa kwao kusafafanizike pamaso panu; pakuti anautsa mkwiyo wanu pamaso pa omanga linga. Koma tinamanga lingali, ndi linga lonse linalumikizana kufikira pakatimpakati; popeza mitima ya anthu inalunjika kuntchito. Koma kunali, atamva Sanibalati, ndi Tobiya, ndi Aarabu, ndi Aamoni, ndi Aasidodi, kuti makonzedwe a malinga a Yerusalemu anakula, ndi kuti mopasuka mwake munayamba kutsekeka, chidawaipira kwambiri; napangana chiwembu iwo onse pamodzi, kudzathira nkhondo ku Yerusalemu, ndi kuchita chisokonezo m'menemo. Koma tinapemphera kwa Mulungu wathu, ndi kuwaikira olindirira usana ndi usiku, chifukwa cha iwowa. Ndipo Ayuda anati, Mphamvu ya osenza akatundu yatha, ndi dothi lichuluka, motero sitidzakhoza kumanga lingali. Nati adani athu, Sadzadziwa kapena kuona mpaka talowa pakati pao, ndi kuwapha, ndi kuleketsa ntchitoyi. Ndipo kunali, atafika Ayuda okhala pafupi pao ochokera pamalo ponse, anatiuza ife kakhumi, Bwererani kwa ife. Chifukwa chake ndinawaika potera m'kati mwa linga, popenyeka; inde ndinaika anthu monga mwa mabanja ao, akhale nao malupanga ao, nthungo zao, ndi mauta ao. Ndipo ndinapenya, ndinanyamuka, ndinanena kwa aufulu, ndi olamulira, ndi anthu otsala, Musamawaopa iwo; kumbukirani Yehova wamkulu ndi woopsa, ndi kuponyera nkhondo abale anu, ana anu aamuna ndi aakazi, akazi anu, ndi nyumba zanu. Ndipo kunali, pakumva adani athu kuti chinadziwika nafe, ndi kuti Mulungu adapititsa pachabe uphungu wao, tinabwera tonse kunka kulinga, yense kuntchito yake. Ndipo kuyambira pamenepo gawo lina la anyamata anga anagwira ntchito, ndi gawo lina linagwira nthungo, zikopa, ndi mauta, ndi malaya achitsulo; ndi akulu anali m'mbuyo mwa nyumba yonse ya Yuda. Iwo omanga linga, ndi iwo osenza katundu, posenza, anachita aliyense ndi dzanja lake lina logwira ntchito, ndi lina logwira chida; ndi omanga linga aliyense anamangirira lupanga lake m'chuuno mwake, nagwira ntchito motero. Ndipo woomba lipenga anali ndi ine. Ndipo ndinati kwa aufulu, ndi olamulira, ndi anthu otsala, Ntchito ndiyo yochuluka ndi yachitando, ndi ife tili palakepalake palingapo, yense atalikizana ndi mnzake; paliponse mukumva mau a lipenga, musonkhanire komweko kwa ife; Mulungu wathu adzatigwirira nkhondo. Momwemo tinalikugwira ntchito; gawo lina la iwo linagwira nthungo kuyambira mbandakucha mpaka zatuluka nyenyezi. Ndinanenanso kwa anthu nthawi yomweyi, Aliyense agone m'Yerusalemu pamodzi ndi mnyamata wake, kuti atilindirire usiku, ndi kugwira ntchito usana. Ndipo ine, ndi abale anga, ndi anyamata anga, angakhale amuna olindirira onditsata ine, nnena mmodzi yense wa ife anavula zovala zake, yense anapita ndi chida chake kumadzi. Pamenepo panamveka kulira kwakukulu kwa anthu ndi akazi ao kudandaula pa abale ao Ayuda. Popeza panali ena akuti, Ife, ana athu aamuna ndi aakazi, ndife ambiri; talandira tirigu, kuti tidye tikhale ndi moyo. Panali enanso akuti, Tili kupereka chikole minda yathu, ndi minda yathu yampesa ndi nyumba zathu; kuti tilandire tirigu chifukwa cha njalayi. Panali enanso akuti, Takongola ndalama za msonkho wa mfumu; taperekapo chikole minda yathu, ndi minda yathu yampesa. Koma tsopano thupi lathu likunga thupi la abale athu, ana athu akunga ana ao; ndipo taonani, titengetsa ana athu aamuna ndi aakazi akhale akapolo, ndi ana athu akazi ena tawatengetsa kale; ndipo tilibe ife mphamvu ya kuchitapo kanthu; ndi minda yathu, ndi minda yathu yampesa, nja ena. Ndipo pakumva kulira kwao, ndi mau ao, kunandiipira kwambiri. Pamenepo mtima wanga unandipangira; ndipo ndinatsutsana nao aufulu ndi olamulira, ndi kunena nao, Mukongoletsa mwa phindu yense kwa mbale wake. Ndipo ndinasonkhanitsa msonkhano waukulu wakuwatsutsa. Ndipo ndinanena nao, Ife monga umo tinakhoza, tinaombola abale athu Ayuda ogulitsidwa kwa amitundu; ndipo kodi inu mukuti mugulitse abale anu, kapena tiwagule ndi ife? Pamenepo anakhala duu, nasowa ponena. Ndinatinso, Chinthu muchitachi si chokoma ai; simuyenera kodi kuyenda m'kuopa Mulungu wathu, chifukwa cha mnyozo wa amitundu, ndiwo adani athu? Kodi ine, ndi abale anga, ndi anyamata anga, tiwakongoletsa ndalama ndi tirigu mwa phindu? Ndikupemphani, tileke phindu ili. Abwezereni lero lomwe minda yao, minda yao yampesa, minda yao ya azitona, ndi nyumba zao, ndi limodzi la magawo zana limodzi la ndalama, ndi tirigu, vinyo, ndi mafuta, limene muwalipitsa. Pamenepo anati, Tidzawabwezera osawalipitsa kanthu, tidzachita monga momwe mwanena. Pamenepo ndinaitana ansembe, ndi kuwalumbiritsa, kuti adzachita monga mwa mau awa. Ndinakutumulanso malaya anga, ndi kuti, Mulungu akutumule momwemo munthu yense wosasunga mau awa, kunyumba yake, ndi kuntchito yake; inde amkutumule momwemo, namtayire zake zonse. Ndi msonkhano wonse unati, Amen, nalemekeza Yehova. Ndipo anthu anachita monga mwa mau awa. Ndipo chiyambire tsiku lija anandiika ndikhale kazembe wao m'dziko la Yuda; kuyambira chaka cha makumi awiri kufikira chaka cha makumi atatu mphambu ziwiri cha Arita-kisereksesi mfumu, ndizo zaka khumi ndi ziwiri, ine ndi abale anga sitinadya chakudya cha kazembe. Koma akazembe akale ndisanakhale ine, analemetsa anthu, nadzitengera kwa iwo mkate, ndi vinyo, pamodzi ndi siliva masekeli makumi anai; angakhale anyamata ao anachita ufumu pa anthu; koma sindinatero ine, chifukwa cha kuopa Mulungu. Ndiponso ndinalimbikira ntchito ya linga ili, ngakhale dziko sitinaligula, ndi anyamata anga onse anasonkhanira ntchito komweko. Panalinso podyera ine Ayuda ndi olamulira amuna zana limodzi mphambu makumi asanu, pamodzi ndi iwo akutidzera kuchokera kwa amitundu otizinga. Zokonzekeratu tsiku limodzi tsono ndizo ng'ombe imodzi, ndi nkhosa zonenepa zisanu ndi imodzi, anandikonzeratunso nkhuku, ndi kamodzi atapita masiku khumi vinyo wambiri wa mitundumitundu; chinkana chonsechi sindinafunsira chakudya cha kazembe, popeza ukapolo unalemerera anthuwo. Mundikumbukire Mulungu, zindikomere zonse ndinachitira anthu awa. Kunali tsono, atamva Sanibalati, ndi Tobiya, ndi Gesemu Mwarabu, ndi adani athu otsala, kuti ndidatha kumanga lingali, posatsalaponso popasuka; (ngakhale pajapo sindinaika zitseko pazipata); anatumiza mau kwa ine Sanibalati ndi Gesemu, kuti, Tiyeni tikomane kumidzi ya ku Chigwa cha Ono; koma analingirira za kundichitira choipa. Ndipo ndinawatumizira mithenga, ndi kuti, Ndilikuchita ntchito yaikulu, sindikhoza kutsika; ndiidulirenji padera ntchito poileka ine, ndi kukutsikirani? Nanditumizira ine mau otere kanai; ndinawabwezeranso mau momwemo. Pamenepo Sanibalati anatuma mnyamata wake kwa ine kachisanu, ndi kalata wosatseka m'dzanja mwake; m'menemo mudalembedwa, Kwamveka mwa amitundu, ndi Gesemu achinena, kuti iwe ndi Ayuda mulikulingirira za kupanduka; chifukwa chake mulikumanga lingali; ndipo iwe udzakhala mfumu yao monga mwa mau awa. Ndiponso waika aneneri akubukitsa za iwe ku Yerusalemu, ndi kuti, Ku Yuda kuli mfumu, ndipo zidzamveka kwa mfumu, kuti kuli zotere. Tiyeni tsono tipangane pamodzi. Koma ndinamtumizira mau, akuti, Palibe zinthu zotere zonga unenazi, koma uzilingirira mumtima mwako. Pakuti anafuna onse kutiopsa, ndi kuti, Manja ao adzaleka ntchito, ndipo siidzachitika. Koma Inu, Mulungu, mulimbitse manja anga tsopano. Pamenepo ndinalowa m'nyumba ya Semaya mwana wa Delaya, mwana wa Mehetabele, wobindikizidwayo, ndipo anati, Tikomane kunyumba ya Mulungu m'kati mwa Kachisi, titsekenso pa makomo a Kachisi; pakuti akudza kudzapha iwe, inde akudza usiku kudzapha iwe. Koma ndinati, Munthu ngati ine nkuthawa kodi? Ndani wonga ine adzalowa m'Kachisi kupulumutsa moyo wake? Sindidzalowamo. Ndipo ndinazindikira kuti sanamtume Mulungu; koma ananena choneneracho pa ine, popeza Tobiya ndi Sanibalati adamlembera. Anamlembera chifukwa cha ichi, kuti ine ndichite mantha, ndi kuchita chotero, ndi kuchimwa; ndi kuti anditolerepo mbiri yoipa ndi kundinyoza. Mukumbukire, Mulungu wanga, Tobiya ndi Sanibalati monga mwa ntchito zao izi, ndi Nowadiya mneneri wamkazi yemwe, ndi aneneri otsala, amene anafuna kundiopsa. Ndipo linga linatsirizika pa tsiku la makumi awiri ndi lachisanu la mwezi wa Eluli, titalimanga masiku makumi asanu mphambu awiri. Ndipo kunali atachimva adani athu onse, amitundu onse akutizinga anaopa, nagwadi nkhope; popeza anazindikira kuti ntchitoyi inachitika ndi Mulungu wathu. Masikuwo aufulu a Yuda analemberanso akalata ambiri kwa Tobiya; ndipo anawafikanso akalata ake a Tobiya. Pakuti ambiri m'Yuda analumbirirana naye chibwenzi; popeza ndiye mkamwini wake wa Sekaniya mwana wa Ara; ndi mwana wake Yehohanani adadzitengera mwana wamkazi wa Mesulamu mwana wa Berekiya. Anatchulanso ntchito zake zokoma pamaso panga namfotokozera iye mau anga. Ndipo Tobiya anatumiza akalata kuti andiopse ine. Ndipo atatha kumanga linga, ndinaika zitseko, nakhazika odikira, ndi oimbira, ndi Alevi; ndipo ndinawapatsa mbale wanga Hanani, ndi Hananiya kazembe wa kuboma, ulamuliro wa pa Yerusalemu; popeza ndiye munthu wokhulupirika, naposa ambiri pakuopa Mulungu. Ndinanenanso nao, Asatsegule pa zipata za Yerusalemu lisanafunde dzuwa; ndi poimirira odikira atseke pazipata, nimuzipiringidze, nimuike alonda mwa iwo okhala m'Yerusalemu, yense polindirira pake, yense pandunji pa nyumba yake. Mudziwo tsono ndi wachitando, ndi waukulu; koma anthu anali m'mwemo ngowerengeka, nyumba zomwe sizinamangike. Ndipo Mulungu wanga anaika m'mtima mwanga kuti ndiwasonkhanitse aufulu, ndi olamulira, ndi anthu, kuti awerengedwe mwa chibadwidwe chao. Ndipo ndinapeza buku la chibadwidwe la iwo adakwerako poyamba paja; ndinapeza mudalembedwa m'mwemo. Ana a dziko amene anakwera kuchokera kundende a iwo adatengedwa ndende, amene Nebukadinezara mfumu ya Babiloni adawatenga, anabwera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, yense kumudzi wake, ndi awa: ndiwo amene anadza ndi Zerubabele: Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Mordekai, Bilisani, Misipereti, Bigivai, Nehumu, Baana. Mawerengedwe a amuna a anthu Aisraele ndiwo: ana a Parosi zikwi ziwiri mphambu zana limodzi kudza makumi asanu ndi awiri. Ana a Sefatiya, mazana atatu mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri. Ana a Ara, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu kudza awiri. Ana a Pahatimowabu, a ana a Yesuwa ndi Yowabu, zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi atatu kudza khumi limodzi ndi asanu ndi atatu. Ana a Elamu, chikwi chimodzi mphambu mazana awiri ndi makumi asanu kudza anai. Ana a Zatu, mazana asanu ndi atatu mphambu makumi anai kudza asanu. Ana a Zakai, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi. Ana a Binuyi, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi anai kudza asanu ndi atatu. Ana a Bebai, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu. Ana a Azigadi, zikwi ziwiri mphambu mazana atatu kudza makumi awiri ndi awiri. Ana a Adonikamu, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi, kudza asanu ndi awiri. Ana a Bigivai, zikwi ziwiri mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi awiri. Ana a Adini, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu kudza asanu. Ana a Atere, a Hezekiya, makumi asanu ndi anai kudza asanu ndi atatu. Ana a Hasumu, mazana atatu mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu. Ana a Bezai, mazana atatu mphambu makumi awiri kudza anai. Ana a Harifi, zana limodzi mphambu khumi ndi awiri. Ana a Gibiyoni, makumi asanu ndi anai kudza asanu. Amuna a ku Betelehemu ndi ku Netofa, zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu kudza asanu ndi atatu. Amuna a ku Anatoti, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu. Amuna a ku Betazimaveti, makumi anai kudza awiri. Amuna a ku Kiriyati-Yearimu, Kefira, ndi Beeroti, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi anai kudza atatu. Amuna a ku Rama ndi Geba, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi awiri kudza mmodzi. Amuna a ku Mikimasi, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza awiri. Amuna a ku Betele ndi Ai, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza atatu. Amuna a ku Nebo winayo, makumi asanu kudza awiri. Ana a Elamu winayo, chikwi chimodzi mphambu mazana awiri ndi makumi asanu kudza anai. Ana a Harimu, mazana atatu mphambu makumi awiri. Ana a Yeriko, mazana atatu mphambu makumi anai kudza asanu. Ana a Lodi, Hadidi, ndi Ono, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi awiri kudza mmodzi. Ana a Senaa, zikwi zitatu mphambu mazana asanu ndi anai kudza makumi atatu. Ansembe: ana a Yedaya, a nyumba ya Yesuwa, mazana asanu ndi anai mphambu makumi asanu ndi awiri kudza atatu. Ana a Imeri, chikwi chimodzi mphambu makumi asanu kudza awiri. Ana a Pasuri, chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi anai ndi asanu ndi awiri. Ana a Harimu, chikwi chimodzi mphambu khumi limodzi kudza asanu ndi awiri. A Levi: ana a Yesuwa, a Kadimiyele, a ana a Hodeva, makumi asanu ndi awiri kudza anai. Oimbira: ana a Asafu, zana limodzi mphambu makumi anai kudza asanu ndi atatu. Odikira: ana a Salumu, ana a Atere, ana a Talimoni, ana a Akubu, ana a Hatita, ana a Sobai, zana limodzi mphambu makumi atatu kudza asanu ndi atatu. Anetini: ana a Ziha, ana a Hasufa, ana a Tabaoti, ana a Kerosi, ana a Siya, ana a Padoni, ana a Lebana, ana a Hagaba, ana a Salimai, ana a Hanani, ana a Gidele, ana a Gahara, ana a Reaya, ana a Rezini, ana a Nekoda, ana a Gazamu, ana a Uza, ana a Paseya, ana a Besai, ana a Meunimu, ana a Nefusesimu, ana a Bakibuki, ana a Hakufa, ana a Harihuri, ana a Baziliti, ana a Mehida, ana a Harisa, ana a Barikosi, ana a Sisera, ana a Tema, ana a Neziya, ana a Hatifa. Ana a akapolo a Solomoni: ana a Sotai, ana a Sofereti, ana a Perida, ana a Yaala, ana a Darikoni, ana a Gidele, ana a Sefatiya, ana a Hatili, ana a Pokereti-Hazebaimu, ana a Amoni. Anetini onse, ndi ana a akapolo a Solomoni, ndiwo mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai kudza awiri. Ndipo okwera kuchokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adoni, ndi Imeri, ndi awa; koma sanakhoze kutchula nyumba za makolo ao, kapena mbumba zao, ngati ali a Israele; ana a Delaya, ana a Tobiya, ana a Nekoda, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi anai kudza awiri. Ndi a ansembe: ana a Hobaya, ana a Hakozi, ana a Barizilai, amene anadzitengera mkazi wa ana akazi a Barizilai Mgiliyadi, natchedwa ndi dzina lao. Awa anafunafuna maina ao m'buku la iwo owerengedwa mwa chibadwidwe, koma osawapeza; potero anawayesa odetsedwa, nawachotsa kuntchito ya nsembe. Ndipo kazembe anawauza kuti asadyeko zopatulika kwambiri, mpaka wauka wansembe wokhala ndi Urimu ndi Tumimu. Msonkhano wonse pamodzi ndiwo zikwi makumi anai ndi ziwiri mphambu mazana atatu kudza makumi asanu ndi limodzi, osawerenga akapolo ao aamuna ndi aakazi, ndiwo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana atatu ndi makumi atatu kudza asanu ndi awiri; ndipo anakhala nao aamuna ndi aakazi oimbira mazana awiri mphambu makumi anai kudza asanu ndi mmodzi. Akavalo ao ndiwo mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu kudza asanu ndi mmodzi; nyuru zao mazana awiri mphambu makumi anai kudza zisanu; ngamira zao mazana anai mphambu makumi atatu kudza asanu; abulu ao zikwi zisanu ndi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi awiri. Ndipo ena a akulu a nyumba za makolo anapereka kuntchito. Kazembeyo anapereka kuchuma madariki agolide chikwi chimodzi, mbale zowazira makumi asanu, malaya a ansembe makumi atatu. Enanso a akulu a nyumba za makolo anapereka kuchuma cha ntchitoyi, madariki agolide zikwi makumi awiri, ndi miyeso ya mina ya siliva zikwi ziwiri mphambu mazana awiri. Zopereka za anthu otsala ndizo madariki agolide zikwi makumi awiri, ndi miyeso ya mina ya siliva zikwi ziwiri, ndi malaya a ansembe makumi asanu ndi limodzi mphambu asanu ndi awiri. Nakhala m'midzi mwao ansembe, ndi Alevi, ndi odikira, ndi oimbira, ndi anthu ena, ndi Anetini, ndi Aisraele onse. Utakhala tsono mwezi wachisanu ndi chiwiri ana a Israele anakhala m'midzi mwao. Ndipo anthu onse anasonkhana ngati munthu mmodzi kukhwalala lili ku Chipata cha Madzi, namuuza Ezara mlembi atenge buku la chilamulo cha Mose, chimene Yehova adalamulira Israele. Ndipo Ezara wansembe anabwera nacho chilamulo pamaso pa msonkhano, ndiwo amuna ndi akazi, ndi yense wakumva ndi kuzindikira tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri. Nawerenga m'menemo pa khwalala lili ku Chipata cha Madzi kuyambira mbandakucha kufikira msana, pamaso pa amuna ndi akazi, ndi iwo okhoza kuzindikira; ndi anthu onse anatcherera khutu buku la chilamulo. Ndipo Ezara mlembi anaima pa chiunda cha mitengo adachimangira msonkhanowo; ndi pambali pake padaima Matitiya, ndi Sema, ndi Anaya, ndi Uriya, ndi Hilikiya, ndi Maaseiya, kudzanja lamanja lake; ndi kudzanja lamanzere Pedaya, ndi Misaele, ndi Malikiya, ndi Hasumu, ndi Hasibadana, Zekariya, ndi Mesulamu. Ndipo Ezara anafunyulula bukulo pamaso pa anthu onse, popeza iye anasomphokera anthu onse; ndipo polifunyulula anthu onse ananyamuka. Pamenepo Ezara analemekeza Yehova Mulungu wamkulu. Navomereza anthu onse, ndi kuti, Amen, Amen; nakweza manja ao, nawerama, nalambira Yehova nkhope zao pansi. Ndi Yesuwa, ndi Bani, ndi Serebiya, Yamini, Akubu, Sabetai, Hodiya, Maaseiya, Kelita, Azariya, Yozabadi, Hanani, Pelaya, ndi Alevi, anadziwitsa anthu chilamulocho; ndi anthu anali chilili pamalo pao. Nawerenga iwo m'buku m'chilamulo cha Mulungu momveka, natanthauzira, nawazindikiritsa chowerengedwacho. Ndipo Nehemiya, ndiye kazembe, ndi Ezara wansembe mlembiyo, ndi Alevi ophunzitsa anthu, ananena ndi anthu onse, Lero ndilo lopatulikira Yehova Mulungu wanu, musamachita maliro, musamalira misozi. Popeza anthu onse analira misozi pakumva mau a chilamulo. Nanena naonso, Mukani, mukadye zonona, mukamwe zozuna, nimumtumizire gawo lake iye amene sanamkonzeretu kanthu; chifukwa lero ndilo lopatulikira Ambuye wathu; ndipo musamachita chisoni; pakuti chimwemwe cha Yehova ndicho mphamvu yanu. Ndipo Alevi anatontholetsa anthu onse, ndi kuti, Khalani muli chete; pakuti lero ndi lopatulika; musamachita chisoni. Napita anthu onse kudya ndi kumwa, ndi kutumiza magawo, ndi kusekerera kwakukulu; popeza anazindikira mau amene adawafotokozera. Ndipo m'mawa mwake akulu a nyumba za makolo a anthu onse, ansembe, ndi Alevi anasonkhana pamodzi kwa Ezara mlembi, kuti atole nzeru za mau a chilamulo. Napeza munalembedwa m'chilamulo kuti Yehova analamulira ndi Mose, kuti ana a Israele azikhala m'misasa pa chikondwerero cha mwezi wachisanu ndi chiwiri, ndi kuti azilalikira ndi kumveketsa m'midzi mwao monse ndi m'Yerusalemu, ndi kuti, Muzitulukira kuphiri, ndi kutengako nthambi za azitona, ndi nthambi za mitengo yamafuta, ndi nthambi za mitengo yamchisu, ndi zinkhwamba za migwalangwa, ndi nthambi za mitengo zothonana, kumanga nazo misasa monga munalembedwa. Natuluka anthu, nakazitenga, nadzimangira misasa, yense pa tsindwi la nyumba yake, ndi m'mabwalo ao, ndi m'mabwalo a nyumba ya Mulungu, ndi pa khwalala la Chipata cha Madzi, ndi pa khwalala la chipata cha Efuremu. Ndi msonkhano wonse wa iwo otuluka m'ndende anamanga misasa, nakhala m'misasamo; pakuti chiyambire masiku a Yoswa mwana wa Nuni kufikira tsiku lija ana a Israele sanatero. Ndipo panali chimwemwe chachikulu. Anawerenganso m'buku la chilamulo cha Mulungu tsiku ndi tsiku, kuyambira tsiku loyamba kufikira tsiku lotsiriza. Nachita chikondwerero masiku asanu ndi awiri; ndi tsiku lachisanu ndi chitatu ndilo msonkhano woletsa, monga mwa malemba. Ndipo tsiku la makumi awiri mphambu anai la mwezi uno ana a Israele anasonkhana ndi kusala, ndi kuvala chiguduli, ndipo anali ndi fumbi. Nadzipatula a mbumba ya Israele kwa alendo onse, naimirira, nawulula zochimwa zao, ndi mphulupulu za makolo ao. Naimirira poima pao, nawerenga m'buku la chilamulo cha Yehova Mulungu wao limodzi la magawo anai a tsiku; ndi limodzi la magawo anai anawulula, napembedza Yehova Mulungu wao. Pamenepo anaimirira pa chiunda cha Alevi Yesuwa, ndi Bani, Kadimiyele, Sebaniya, Buni, Serebiya, Bani, ndi Kenani, nafuula ndi mau akulu kwa Yehova Mulungu wao. Nati Alevi, Yesuwa, ndi Kadimiyele, Bani, Hasabineya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya, ndi Petahiya, Imirirani, lemekezani Yehova Mulungu wanu kunthawi za nthawi; ndipo lilemekezeke dzina lanu la ulemerero, lokuzika loposa chilemekezo ndi chiyamiko chonse. Inu ndinu Yehova, nokhanu; mwalenga thambo, kumwambamwamba, ndi khamu lao lonse, dziko lapansi, ndi zonse zili pomwepo, nyanja ndi zonse zili m'mwemo, ndi Inu muzisunga zamoyo zonsezi, ndi khamu lakumwamba lilambira Inu. Inu ndinu Yehova Mulungu amene munasankha Abramu ndi kumtulutsa m'Uri wa Ababiloni, ndi kumutcha dzina lake Abrahamu; ndipo munampeza mtima wake wokhulupirika pamaso panu, nimunapangana naye kumpatsa dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, ndi Aperizi, ndi Ayebusi, ndi Agirigasi, kulipereka kwa mbumba zake; ndipo mwakwaniritsa mau anu, popeza Inu ndinu wolungama. Ndipo munapenya msauko wa makolo athu m'Ejipito, nimunamva kufuula kwao ku Nyanja Yofiira, nimunachitira zizindikiro ndi zodabwitsa Farao ndi akapolo ake onse, ndi anthu onse a m'dziko lake; popeza munadziwa kuti anawachitira modzikuza; ndipo munadzibukitsira dzina monga lero lino. Ndipo munagawanitsa nyanja pamaso pao, napita iwo pakati pa nyanja pouma, ndipo munaponya mozama owalondola, ngati mwala m'madzi olimba. Munawatsogoleranso usana ndi mtambo woti njo, ndi moto tolo usiku, kuwaunikira m'njira akayendamo. Munatsikiranso pa phiri la Sinai, nimunalankhula nao mochokera m'Mwamba, ndipo munawapatsa maweruzo oyenera, ndi chilamulo choona, malemba, ndi malamulo okoma; ndi Sabata lanu lopatulika munawadziwitsa, nimunawalamulira malamulo, ndi malemba, ndi chilamulo, mwa dzanja la Mose mtumiki wanu; ndi mkate wochokera m'mwamba munawapatsa pa njala yao; ndi madzi otuluka m'thanthwe munawatulutsira pa ludzu lao, ndi kuwauza alowe, nalandire dziko limene mudakwezapo dzanja lanu kuwapatsa. Koma iwo ndi makolo athu anachita modzikuza, naumitsa khosi lao, osamvera malamulo anu, nakana kumvera, osakumbukiranso zodabwitsa zanu munazichita pakati pao; koma anaumitsa khosi lao, ndipo m'kupanduka kwao anaika mtsogoleri abwerere kunka ku ukapolo wao; koma Inu ndinu Mulungu wokhululukira, wachisomo, ndi wansoni, wolekereza, ndi wochuluka chifundo; ndipo simunawasiya. Ngakhale apa atadzipangira mwanawang'ombe woyenga, nati, Suyu Mulungu wako anakukweza kuchokera ku Ejipito, nachita zopeputsa zazikulu; koma Inu mwa nsoni zanu zazikulu simunawasiya m'chipululu; mtambo woti njo sunawachokera usana kuwatsogolera m'njira, ngakhale moto wa tolo usiku kuwaunikira panjira anayenera kuyendamo. Munawapatsanso mzimu wanu wokoma kuwalangiza, ndipo simunawamana mana anu pakamwa pao; munawapatsanso madzi pa ludzu lao. Ndipo munawalera zaka makumi anai m'chipululu, osasowa kanthu iwo; zovala zao sizinatha, ndi mapazi ao sanatupe. Munawapatsanso maufumu, ndi mitundu ya anthu, nimunawagawa m'madera, motero analandira likhale laolao dziko la Sihoni, ndilo dziko la mfumu ya ku Hesiboni, ndi dziko la Ogi mfumu ya ku Basani. Ana aonso munawachulukitsa monga nyenyezi za m'mwamba, nimunawalowetsa m'dziko mudalinena kwa makolo ao, alowemo likhale laolao. Nalowa anawo, nalandira dzikoli likhale laolao, ndipo munagonjetsa pamaso pao okhala m'dziko, ndiwo Akanani, ndi kuwapereka m'dzanja mwao, pamodzi ndi mafumu ao, ndi mitundu ya anthu ya m'dziko, kuti achite nao chifuniro chao. Ndipo analanda midzi yamalinga, ndi dziko la zonona, nalandira zikhale zaozao nyumba zodzala ndi zokoma zilizonse, zitsime zokumbidwa, minda yampesa, ndi minda ya azitona, ndi mitengo yambiri yazipatso; nadya iwo, nakhuta, nanenepa, nakondwera nako kukoma kwanu kwakukulu. Koma anakhala osamvera, napandukira Inu, nataya chilamulo chanu m'mbuyo mwao napha aneneri anu akuwachitira umboni, kuwabwezera kwa Inu, nachita zopeputsa zazikulu. Chifukwa chake munawapereka m'dzanja la adani ao akuwasautsa; koma mu nthawi ya kusautsika kwao anafuula kwa Inu, ndipo munamva m'Mwamba, ndi monga mwa nsoni zanu zambiri munawapatsa apulumutsi akuwapulumutsa m'dzanja la adani ao. Koma atapumula, anabwereza kuchita choipa pamaso panu; chifukwa chake munawasiya m'dzanja la adani ao amene anachita ufumu pa iwo; koma pobwera iwo ndi kufuula kwa Inu, munamva m'Mwamba ndi kuwapulumutsa kawirikawiri, monga mwa chifundo chanu; ndipo munawachitira umboni, kuti muwabwezerenso ku chilamulo chanu; koma anachita modzikuza, osamvera malamulo anu; koma anachimwira malamulo anu (amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo); nakaniza phewa lao, naumitsa khosi lao, osamvera. Koma munawalekerera zaka zambiri, ndi kuwachitira umboni ndi mzimu wanu, mwa aneneri anu, koma sanamvere; chifukwa chake munawapereka m'dzanja la mitundu ya anthu a m'dziko. Ndipo mwa nsoni zanu zochuluka simunawatha, kapena kuwataya; popeza Inu ndinu Mulungu wa chisomo ndi chifundo. Ndipo tsono, Mulungu wathu, ndinu Mulungu wamkulu, ndi wamphamvu, ndi woopsa, wakusunga pangano ndi chifundo, asachepe pamaso panu mavuto athu onse amene anatigwera ife, ndi mafumu athu, akulu athu, ndi ansembe athu, ndi aneneri athu, ndi makolo athu, ndi anthu anu onse, kuyambira masiku a mafumu a Asiriya, mpaka lero lino. Koma Inu ndinu wolungama mwa zonse zatigwera; pakuti mwachita zoona, koma ife tachita choipa; ndi mafumu athu, akulu athu, ansembe athu, ndi makolo athu, sanasunge chilamulo chanu, kapena kumvera malamulo anu, ndi mboni zanu, zimene munawachitira umboni nazo. Popeza sanatumikire Inu m'ufumu wao, ndi m'ubwino wanu wochuluka umene mudawapatsa, ndi m'dziko lalikulu ndi la zonona mudalipereka pamaso pao, ndipo sanabwerere kuleka ntchito zao zoipa. Tapenyani, ife lero ndife akapolo, ndi dzikoli mudalipereka kwa makolo athu kudya zipatso zake ndi zokoma zake, taonani, ife ndife akapolo m'menemo. Ndipo lichulukitsira mafumu zipatso zake, ndiwo amene munawaika atiweruze, chifukwa cha zoipa zathu; achitanso ufumu pa matupi athu, ndi pa zoweta zathu, monga umo akonda; ndipo ife tisauka kwakukulu. Ndipo mwa ichi chonse tichita pangano lokhazikika, ndi kulilemba, ndi akulu athu, Alevi athu, ndi ansembe athu, alikomera chizindikiro. Okomera chizindikiro tsono ndiwo Nehemiya, Tirisata mwana wa Hakaliya, ndi Zedekiya, Seraya, Azariya, Yeremiya, Pasuri, Amariya, Malikiya, Hatusi, Sebaniya, Maluki, Harimu, Meremoti, Obadiya, Daniele, Ginetoni, Baruki, Mesulamu, Abiya, Miyamini, Maaziya, Biligai, Semaya, ndiwo ansembe. Ndi Alevi ndiwo Yesuwa mwana wa Azaniya, Binuyi wa ana a Henadadi, Kadimiyele; ndi abale ao: Sebaniya, Hodiya, Kelita, Pelaya, Hanani, Mika, Rehobu, Hasabiya, Zakuri, Serebiya, Sebaniya, Hodiya, Bani, Beninu. Akulu a anthu: Parosi, Pahatimowabu, Elamu, Zatu, Bani, Buni, Azigadi, Bebai, Adoniya, Bigivai, Adini, Atere, Hezekiya, Azuri, Hodiya, Hasumu, Bezai, Harifi, Anatoti, Nebai, Magapiyasi, Mesulamu, Heziri, Mesezabele, Zadoki, Yaduwa, Pelatiya, Hanani, Anaya, Hoseya, Hananiya, Hasubu, Halohesi, Piliha, Sobeki, Rehumu, Hasabuna, Maaseiya, ndi Ahiya, Hanani, Anani, Maluki, Harimu, Baana. Ndi anthu otsala, ansembe, Alevi, odikira, oimbira, Anetini, ndi onse anadzisiyanitsawo pa mitundu ya anthu a m'dziko kutsata chilamulo cha Mulungu, akazi ao, ana ao aamuna ndi aakazi, yense wodziwa ndi wozindikira, amenewa anaumirira abale ao, omveka ao, nalowa m'temberero ndi lumbiro, kuti adzayenda m'chilamulo cha Mulungu anachipereka Mose mtumiki wa Mulungu, ndi kuti adzasunga ndi kuchita zonse atilamulira Yehova Ambuye wathu, ndi maweruzo ake, ndi malemba ake; ndi kuti sitidzapereka ana athu akazi kwa mitundu ya anthu a m'dziko, kapena kutengera ana athu amuna ana ao akazi; ndipo mitundu ya anthu a m'dziko akabwera nao malonda, ngakhale tirigu, tsiku la Sabata, kutsata malonda, sitidzagulana nao tsiku la Sabata, kapena dzuwa lina lopatulika, ndi kuti tidzaleka chaka chachisanu ndi chiwiri ndi mangawa ali onse. Tinadziikiranso malamulo, kuti tizipereka chaka ndi chaka limodzi la magawo atatu a sekeli kuntchito ya nyumba ya Mulungu wathu; kulipereka mkate woonekera, ndi nsembe yaufa yosaleka, ndi nsembe yopsereza yosaleka, ya masabata, ya pokhala miyezi, kuliperekera nyengo zoikika ndi zopatulikira, ndi nsembe za zolakwa za kutetezera Israele zoipa, ndi ntchito zonse za nyumba ya Mulungu wathu. Ndipo tinalota maere, ansembe, Alevi, ndi anthu, a chopereka cha nkhuni, kubwera nazo kunyumba ya Mulungu wathu, monga mwa nyumba za makolo athu, pa nyengo zoikika chaka ndi chaka, kuzisonkha pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu, monga mulembedwa m'chilamulo; ndi kubwera nazo zipatso zoyamba za nthaka, ndi zoyamba za zipatso zonse za mtengo uliwonse chaka ndi chaka, ku nyumba ya Yehova; ndi ana athu oyamba kubadwa, ndi oyamba kubadwa a nyama zathu, monga mulembedwa m'chilamulo, ndi oyamba a ng'ombe zathu, ndi nkhosa zathu, kubwera nazo kunyumba ya Mulungu wathu kwa ansembe akutumikira m'nyumba ya Mulungu wathu; ndi kuti tidzabwera nazo za mtanda wa mkate wathu woyamba, ndi nsembe zathu zokwera, ndi zipatso za mtengo uliwonse, vinyo, ndi mafuta, kwa ansembe, kuzipinda za nyumba ya Mulungu wathu; ndi limodzi la magawo khumi la nthaka yathu kwa Alevi; pakuti Alevi amene amalandira limodzilimodzi la magawo khumi m'midzi yonse yolima ife. Ndipo wansembe mwana wa Aroni azikhala ndi Alevi, polandira Alevi limodzilimodzi la magawo khumi; ndi Alevi azikwera nalo limodzi la magawo khumi mwa limodzilimodzi la magawo khumi kunyumba ya Mulungu wathu, kuzipinda, kunyumba ya chuma. Pakuti ana a Israele ndi ana a Levi, azibwera nayo nsembe yokweza yatirigu, ndi yavinyo ndi yamafuta, kuzipinda kuli zipangizo za malo opatulika, ndi ansembe akutumikira, ndi odikira, ndi oimbira; kuti tisasiye nyumba ya Mulungu wathu. Ndipo akulu a anthu anakhala m'Yerusalemu; anthu otsala omwe anachita maere, kuti libwere limodzi la magawo khumi likhale m'Yerusalemu, mudzi wopatulika, ndi asanu ndi anai akhumi m'midzi ina. Ndipo anthu anadalitsa amuna onse akudzinenera mwaufulu kuti adzakhala m'Yerusalemu. Awa tsono ndi akulu a dziko okhala m'Yerusalemu; koma m'midzi ya Yuda yense anakhala pa cholowa chake m'midzi mwao, ndiwo Israele, ansembe, ndi Alevi, ndi Anetini, ndi ana a akapolo a Solomoni. Ndipo m'Yerusalemu munakhala ena a ana a Yuda ndi ana a Benjamini. Mwa ana a Yuda: Ataya mwana wa Uziya, mwana wa Zekariya, mwana wa Amariya, mwana wa Sefatiya, mwana wa Mahalalele, wa ana a Perezi; ndi Maaseiya mwana wa Baruki, mwana wa Kolihoze, mwana wa Hazaya, mwana wa Adaya, mwana wa Yoyaribu, mwana wa Zekariya, mwana wa Msiloni. Ana onse a Perezi okhala m'Yerusalemu ndiwo ngwazi mazana anai mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi atatu. Ndi ana a Benjamini ndi awa: Salu mwana wa Mesulamu, mwana wa Yoedi, mwana wa Pedaya, mwana wa Kolaya, mwana wa Maaseiya, mwana wa Itiyele, mwana wa Yesaya. Ndi wotsatana naye Gabai, Salai, mazana asanu ndi anai mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu. Ndi Yowele mwana wa Zikiri ndiye woyang'anira wao, ndi Yuda mwana wa Hasenuwa ndiye wothandizana naye, poyang'anira mudzi. Mwa ansembe: Yedaya mwana wa Yoyaribu, Yakini, Seraya mwana wa Hilikiya, mwana wa Mesulamu, mwana wa Zadoki, mwana wa Meraiyoti, mwana wa Ahitubi mtsogoleri wa m'nyumba ya Mulungu; ndi abale ao ochita ntchito ya m'nyumbayi ndiwo mazana asanu ndi atatu mphambu makumi awiri kudza awiri; ndi Adaya mwana wa Yerohamu, mwana wa Pelaliya, mwana wa Amizi, mwana wa Zekariya, mwana wa Pasuri, mwana wa Malikiya; ndi abale ake akulu a nyumba za makolo awiri mphambu makumi anai kudza awiri, ndi Amasisai mwana wa Azarele, mwana wa Ahazai, mwana wa Mesilemoti, mwana wa Imeri; ndi abale ao, ngwazi zamphamvu, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu; ndi woyang'anira wao ndiye Zabidiele mwana wa Hagedolimu. Ndi mwa Alevi: Semaya mwana wa Hasubu, mwana wa Azirikamu, mwana wa Hasabiya, mwana wa Buni; ndi Sabetai, ndi Yozabadi, mwa akulu a Alevi, anayang'anira ntchito za pabwalo za nyumba ya Mulungu; ndi Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zabidi, mwana wa Asafu, ndiye mkulu wakuyamba mayamiko, popemphera; ndi Bakibukiya wotsatana naye mwa abale ake, ndi Abida mwana wa Samuwa, mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni. Alevi onse m'mudzi wopatulikawo ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu kudza anai. Ndi odikira: Akubu, Talimoni, ndi abale ao akulindira pazipata, ndiwo zana limodzi mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri. Ndi Aisraele otsala ndiwo ansembe ndi Alevi, anakhala m'midzi yonse ya Yuda, yense m'cholowa chake. Koma Anetini anakhala m'Ofele, ndi Ziha, ndi Gisipa anali oyang'anira Anetini. Ndipo woyang'anira wa Alevi m'Yerusalemu ndiye Uzi mwana wa Bani, mwana wa Hasabiya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mika; mwa ana a Asafu oimbira ena anayang'anira ntchito ya m'nyumba ya Mulungu. Pakuti mfumu inalamulira za iwowa, naikira oimbira chowathandiza, yense chake pa tsiku lake. Ndi Petahiya mwana wa Mesezabele, wa ana a Zera, mwana wa Yuda, anatumikira mfumu pa milandu yonse ya anthuwo. Ndi ana ena a Yuda anakhala m'midzi ya kuminda yao, m'Kiriyati-Ariba ndi milaga yake, ndi m'Diboni ndi milaga yake, ndi m'Yekabizeele ndi midzi yake, ndi m'Yesuwa, ndi m'Molada, ndi Betepeleti, ndi m'Hazara-Suwala, ndi m'Beereseba ndi milaga yake, ndi m'Zikilagi, ndi m'Mekona ndi milaga yake, ndi m'Enirimoni, ndi m'Zora, ndi m'Yaramuti, Zanowa, Adulamu ndi midzi yao, Lakisi ndi minda yake, Azeka ndi milaga yake. Ndipo anamanga misasa kuyambira ku Beereseba mpaka chigwa cha Hinomu. Ana a Benjamini omwe, kuyambira ku Geba pa Mikimasi, ndi Aya, ndi pa Betele ndi milaga yake, pa Anatoti, Nobi, Ananiya, Hazori, Rama, Gitaimu, Hadidi, Zeboimu, Nebalati, Lodi, ndi Ono, chigwa cha amisiri. Ndi magawo a Levi anakhala ena ku Yuda, ndi ena ku Benjamini. Ndipo ansembe ndi Alevi amene anakwera ndi Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yesuwa, ndi awa: Seraya, Yeremiya, Ezara, Amariya, Maluki, Hatusi, Sekaniya, Rehumu, Meremoti, Ido, Ginetoyi, Abiya, Miyamini, Maadiya, Biliga, Semaya, ndi Yoyaribu, Yedaya. Salu, Amoki, Hilikiya, Yedaya. Awa ndi akulu a ansembe ndi abale ao m'masiku a Yesuwa. Ndi Alevi ndiwo Yesuwa, Binuyi, Kadimiyele, Serebiya, Yuda, ndi Mataniya; iye ndi abale ake amatsogolera mayamiko. Ndi Bakibukiya ndi Uni, abale ao, anawayang'anira maulonda. Ndi Yesuwa anabala Yoyakimu, ndi Yoyakimu anabala Eliyasibu ndi Eliyasibu anabala Yoyada, ndi Yoyada anabala Yonatani, ndi Yonatani, anabala Yaduwa. Ndi m'masiku a Yoyakimu ansembe aakulu a nyumba za makolo ndiwo: wa Seraya, Meraya; wa Yeremiya, Hananiya; wa Ezara, Mesulamu; wa Amariya, Yehohanani; wa Maluki, Yonatani; wa Sebaniya, Yosefe; wa Harimu, Adina; wa Meraiyoti, Helikai; wa Ido, Zekariya; wa Ginetoni, Mesulamu; wa Abiya, Zikiri; wa Miniyamini, wa Mowadiya, Pilitai; wa Biliga, Samuwa; wa Semaya, Yehonatani; ndi wa Yoyaribu, Matenai; wa Yedaya, Uzi; wa Salai, Kalai; wa Amoki, Eberi; wa Hilikiya, Hasabiya; wa Yedaya, Netanele. M'masiku a Eliyasibu, Yoyada, Yohanani, ndi Yaduwa, Alevi analembedwa akulu a nyumba za makolo; ansembe omwe, mpaka ufumu wa Dariusi wa ku Persiya. Ana a Levi, akulu a nyumba za makolo, analembedwa m'buku la machitidwe, mpaka masiku a Yohanani mwana wa Eliyasibu. Ndi akulu a Alevi: Hasabiya, Serebiya, ndi Yesuwa mwana wa Kadimiyele, ndi abale ao openyana nao, kulemekeza ndi kuyamika, monga mwa lamulo la Davide munthu wa Mulungu, alonda kupenyana alonda. Mataniya, ndi Bakibukiya, Obadiya, Mesulamu, Talimoni, Akubu, ndiwo odikira akulonda pa nyumba za chuma zili kuzipata. Awa anakhala m'masiku a Yoyakimu mwana wa Yesuwa, mwana wa Yozadaki, ndi m'masiku a Nehemiya kazembe, ndi a Ezara wansembe mlembiyo. Ndipo popereka linga la Yerusalemu anafunafuna Alevi m'malo mwao monse, kubwera nao ku Yerusalemu, kuti achite kuperekaku mokondwera, ndi mayamiko, ndi kuimbira, ndi nsanje, zisakasa, ndi azeze. Ana a oimbirawo anasonkhana ochokera ku dziko lozungulira Yerusalemu, ndi kumidzi ya Anetofa, ndi ku Betegiligala, ndi ku minda ya Geba ndi Azimaveti; popeza oimbirawo adadzimangira midzi pozungulira Yerusalemu. Ndipo ansembe ndi Alevi anadziyeretsa okha, nayeretsa anthu, ndi zipata, ndi linga. Pamenepo ndinakwera nao akulu a Yuda pa lingali, ndinaikanso oyamikira magulu awiri akulu oyenda molongosoka; lina loyenda ku dzanja lamanja palinga kunka ku Chipata cha Kudzala; ndi pambuyo pao anayenda Hosaya, ndi limodzi la magawo awiri a akulu a Yuda, ndi Azariya, Ezara ndi Mesulamu, Yuda, ndi Benjamini, ndi Semaya, ndi Yeremiya, ndi ana ena a ansembe ndi malipenga: Zekariya mwana wa Yonatani, mwana wa Semaya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mikaya, mwana wa Zakuri, mwana wa Asafu, ndi abale ake: Semaya, ndi Azarele, Milalai, Gilalai, Maai, Netanele, ndi Yuda, Hanani, ndi zoimbira za Davide munthu wa Mulungu; ndi Ezara mlembiyo anawatsogolera; ndi ku Chipata cha ku Chitsime, ndi kundunji kwao, anakwerera pa makwerero a mudzi wa Davide, potundumuka linga, popitirira pa nyumba ya Davide, mpaka ku Chipata cha Madzi kum'mawa. Ndi gulu lina la oyamikira linamuka mokomana nao, ndi ine ndinawatsata, pamodzi ndi limodzi la magawo awiri la anthu palinga, napitirira pa Nsanja ya Ng'anjo, mpaka kulinga lachitando; ndi pamwamba pa Chipata cha Efuremu, ndi ku Chipata Chakale, ndi ku Chipata Chansomba, ndi Nsanja ya Hananele, ndi Nsanja ya Zana, mpaka kuchipata chankhosa; ndipo anaima ku Chipata cha Akaidi. Atatero, magulu awiriwo a iwo oyamikira anaima m'nyumba ya Mulungu, ndipo ine ndi limodzi la magawo awiri a olamulira pamodzi ndi ine; ndi ansembe, Eliyakimu, Maaseiya, Miniyamini, Mikaya, Eliyoenai, Zekariya, ndi Hananiya, ali nao malipenga; ndi Maaseiya, ndi Semaya, ndi Eleazara, ndi Uzi, ndi Yehohanani, ndi Malikiya, ndi Elamu, ndi Ezere. Ndipo oimbira anaimbitsa Yezeraya ndiye woyang'anira wao. Ndipo anaphera nsembe zambiri tsiku lija, nasekerera; pakuti Mulungu anawakondweretsa ndi chimwemwe chachikulu; ndi akazi omwe ndi ana anakondwera; ndi chikondwerero cha Yerusalemu chinamveka kutali. Ndipo tsiku lomwelo anaika anthu asunge zipinda za chuma, za nsembe zokweza, za zipatso zoyamba, ndi za limodzilimodzi la magawo khumi, kulonga m'mwemo, monga mwa minda ya midzi, magawo onenedwa ndi chilamulo, akhale a ansembe ndi Alevi; popeza Yuda anakondwera nao ansembe ndi Alevi akuimirirako. Ndipo iwo anasunga udikiro wa Mulungu wao, ndi udikiro wa mayeretsedwe; momwemonso oimbira ndi odikira, monga mwa lamulo la Davide ndi la Solomoni mwana wake. Pakuti m'masiku a Davide ndi Asafu kalelo kunali mkulu wa oimbira, ndi wa nyimbo zolemekeza ndi zoyamikira Mulungu. Ndi Aisraele onse m'masiku a Zerubabele, ndi m'masiku a Nehemiya, anapereka magawo a oimbira ndi odikira, monga mudafunika tsiku ndi tsiku; nawapatulira Alevi; ndi Alevi anawapatulira ana a Aroni. Tsiku lomwelo anawerenga m'buku la Mose m'makutu a anthu, napeza m'menemo kuti Aamoni ndi Amowabu asalowe mu msonkhano wa Mulungu kunthawi yonse; popeza sanawachingamire ana a Israele ndi chakudya ndi madzi, koma anawalemberera Balamu awatemberere; koma Mulungu wathu anasanduliza tembererolo likhale mdalitso. Ndipo kunali, atamva chilamulocho, anasiyanitsa pa Israele anthu osokonezeka onse. Chinkana ichi, Eliyasibu wansembe, woikidwa asunge zipinda za nyumba ya Mulungu wathu, anachita chibale ndi Tobiya, namkonzera chipinda chachikulu, kumene adasungira kale zopereka za ufa, lubani, ndi zipangizo, ndi limodzilimodzi la magawo khumi a tirigu, vinyo, ndi mafuta, zolamulidwira Alevi, ndi oimbira, ndi odikira, ndi nsembe zokweza za ansembe. Koma pochitika ichi chonse sindinakhala ku Yerusalemu; pakuti chaka cha makumi atatu ndi chachiwiri cha Arita-kisereksesi mfumu ya Babiloni ndinafika kwa mfumu, ndipo atapita masiku ena ndinapempha mfumu indilole; ndipo ndinafika ku Yerusalemu, ndi kuzindikira choipa anachichita Eliyasibu, chifukwa cha Tobiya, ndi kumkonzera chipinda m'mabwalo a nyumba ya Mulungu. Ndipo ndinaipidwa nacho kwambiri, motero ndinataya kubwalo akatundu onse a m'nyumba ya Tobiya, kuwachotsa m'chipindamo. Pamenepo ndinalamulira, ndipo anayeretsa zipindazo; ndipo ndinabwezeramonso zipangizo za nyumba ya Mulungu, pamodzi ndi zopereka za ufa ndi lubani. Ndinazindikiranso kuti sanapereke kwa Alevi magawo ao; m'mwemo Alevi ndi oimbira adathawira yense kumunda wake. Potero ndinatsutsana nao olamulira, ndinati, Yasiyidwiranji nyumba ya Mulungu? Ndipo ndinawasonkhanitsa, ndi kuwaika m'malo mwao. Ndi Ayuda onse anabwera nalo limodzilimodzi la magawo khumi a tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, kunyumba za chuma. Ndinaikanso osunga chuma: Selemiya wansembe, ndi Zadoki mlembi; ndi wa Alevi, Pedaya; ndi wakuwathandiza, Hanani mwana wa Zakuri, mwana wa Mataniya; popeza anayesedwa okhulupirika ndi udindo wao, ndiwo kugawira abale ao. Mundikumbukire Mulungu wanga mwa ichi, nimusafafanize zokoma zanga ndinazichitira nyumba ya Mulungu wanga, ndi maudikiro ake. Masiku awa ndinaona ku Yuda ena akuponda mphesa m'choponderamo tsiku la Sabata, ndi akubwera nayo mitolo ya tirigu, ndi kuisenzetsa pa abulu; momwemonso vinyo, mphesa, ndi nkhuyu, ndi zosenza zilizonse, zimene analowa nazo m'Yerusalemu tsiku la Sabata, ndipo ndinawachitira umboni wakuwatsutsa tsikuli anagulitsa zakudya. Anakhalanso m'menemo a ku Tiro, obwera nazo nsomba, ndi malonda ali onse, nagulitsa tsiku la Sabata kwa ana a Yuda ndi m'Yerusalemu. Pamenepo ndinatsutsana nao aufulu a Yuda, ndinanena nao, Chinthu chanji choipa ichi muchichita, ndi kuipsa nacho tsiku la Sabata? Sanatero kodi makolo anu, ndipo Mulungu wathu anatifikitsira ife ndi mudzi uno choipa ichi chonse? Koma inu muonjezera Israele mkwiyo pakuipsa Sabata. Ndipo kunali, kukadayamba chizirezire pa zipata za Yerusalemu, losafika Sabata, ndinawauza atseke pamakomo; ndinawauzanso kuti asatsegulepo, koma litapita Sabata ndipo; ndipo ndinaimika anyamata anga ena pazipata, kuti pasalowe katundu tsiku la Sabata. Momwemo eni malonda ndi ogulitsa malonda ali onse, anagona kunja kwa Yerusalemu kamodzi kapena kawiri. Koma ndinawachitira umboni wakuwatsutsa, ndinanena nao, Mugoneranji pafupi pa linga? Mukateronso ndikuthirani manja. Kuyambira pomwepo sanafikenso pa Sabata. Ndipo ndinauza Alevi kuti adziyeretse, nabwere, nasunge pazipata kupatula tsiku la Sabata. Mundikumbukire ichinso, Mulungu wanga, ndi kundileka monga mwa chifundo chanu chachikulu. Masiku aja ndinaonanso Ayudawo anadzitengera akazi a Asidodi, Aamoni, ndi Amowabu, ndi ana ao analankhula mwina Chiasidodi, osadziwitsa kulankhula Chiyuda, koma monga umo amalankhula mtundu wao uliwonse. Ndipo ndinatsutsana nao, ndi kuwatemberera, ndi kukantha ena a iwo, ndi kumwetula tsitsi lao, ndi kuwalumbiritsa pa Mulungu ndi kuti, Musapereka ana anu akazi kwa ana ao amuna, kapena kutengera ana anu amuna, kapena a inu nokha, ana ao akazi. Nanga Solomoni mfumu ya Israele sanachimwe nazo zinthu izi? Chinkana mwa amitundu ambiri panalibe mfumu ngati iye, ndi Mulungu wake anamkonda, ndi Mulungu wake anamlonga mfumu ya Aisraele onse; koma ngakhale iye, akazi achilendo anamchimwitsa. Ndipo kodi tidzamvera inu, kuchita choipa ichi chachikulu chonse, kulakwira Mulungu wathu ndi kudzitengera akazi achilendo? Koma wina wa ana a Yehoyada, mwana wa Eliyasibu mkulu wa ansembe, anali mkamwini wa Sanibalati Muhoroni; chifukwa chake ndinampirikitsa kumchotsa kwa ine. Muwakumbukire Mulungu wanga, popeza anadetsa unsembe, ndi pangano la unsembe, ndi la Alevi. Momwemo ndinawayeretsa kuwachotsera achilendo onse, ndi kuikira udikiro ansembe ndi Alevi, yense kuntchito yake; ndi chopereka cha nkhuni pa nthawi zoikika, ndi wa zipatso zoyamba. Mundikumbukire, Mulungu wanga, chindikomere. Izi zinachitika masiku a Ahasuwero, ndiye Ahasuweroyo anachita ufumu kuyambira Indiya kufikira Kusi, pa maiko zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi awiri. Masiku ajawo, pokhala Ahasuwero pa mpando wa ufumu wake uli m'chinyumba cha ku Susa, chaka chachitatu cha ufumu wake, anakonzera madyerero akalonga ake onse, ndi omtumikira; amphamvu a Persiya ndi Mediya, omveka ndi akalonga a maikowo anakhala pamaso pake, pamene anaonetsa zolemera za ufumu wake waulemu, ndi ulemerero wa ukulu wake woposa, masiku ambiri, ndiwo masiku zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu. Atatha masikuwa, mfumu inakonzera madyerero anthu onse okhala m'chinyumba cha ku Susa, akulu ndi ang'ono, masiku asanu ndi awiri, ku bwalo la munda wa maluwa wa ku chinyumba cha mfumu; panali nsalu zolenjeka zoyera, zabiriwiri, ndi zamadzi, zomangika ndi zingwe za thonje labafuta, ndi lofiirira, pa zigwinjiri zasiliva, ndi nsanamira zansangalabwi; makama anali a golide ndi siliva pa mayalidwe a miyala yofiira, ndi yoyera, ndi yoyezuka, ndi yakuda. Nawapatsa chakumwa m'zomwera zagolide, zomwerazo nzosiyanasiyana, ndi vinyo wachifumu anachuluka, monga mwa ufulu wa mfumu. Ndi mamwedwewo anali monga mwa lamulo; panalibe kukakamiza; pakuti mfumu idaikira akulu onse a nyumba yake motero, kuti achite monga momwe akhumba aliyense. Vasiti yemwe, mkazi wamkulu, anakonzera akazi madyerero m'nyumba yachifumu ya mfumu Ahasuwero. Tsiku lachisanu ndi chiwiri, pokondwera mtima wa mfumu ndi vinyo, iye anauza Mehumani, Bizita, Haribona, Bigita, ndi Abagita, Zetara, ndi Karikasi, adindo asanu ndi awiriwo akutumikira pamaso pa mfumu Ahasuwero, abwere naye Vasiti mkazi wamkulu pamaso pa mfumu ndi korona wachifumu, kuonetsa anthu ndi akulu kukoma kwake; popeza anali wokongola maonekedwe ake. Koma Vasiti mkazi wamkuluyo anakana kudza pa mau a mfumu adamuuza adindowo; potero mfumu idapsa mtima ndithu, ndi mkwiyo wake unatentha m'kati mwake. Pamenepo mfumu inanena kwa eni nzeru, akudziwa za m'tsogolo, mfumu idafotero nao onse akudziwa malamulo ndi maweruzo, a pafupi naye ndiwo Karisena, Setara, Adimata, Tarisisi, Meresi, Marisena, ndi Memukana, akalonga asanu ndi awiri a Persiya ndi Mediya, openya nkhope ya mfumu ndi kukhala oyamba m'ufumu. Anati, Tidzachitanji naye mkazi wamkulu Vasiti monga mwa malamulo, popeza sanachite chomuuza mfumu Ahasuwero mwa adindo? Ndi Memukana anati, pamaso pa mfumu ndi akalonga, Vasiti mkazi wamkulu sanalakwire mfumu yekha, komanso akalonga onse, ndi mitundu yonse ya anthu okhala m'maiko onse a mfumu Ahasuwero. Pakuti machitidwe awa a mkazi wamkuluyo adzabuka kufikira akazi onse, kupeputsa amuna ao pamaso pao; anthu akati, Mfumu Ahasuwero anati abwere naye Vasiti mkazi wamkulu pamaso pake, koma sanadze iye. Inde tsiku lomwelo akazi akulu a Persiya ndi Mediya, atamva machitidwe a mkazi wamkuluyo, adzatero nao momwemo kwa akalonga onse a mfumu. Ndi chipeputso ndi mkwiyo zidzachuluka. Chikakomera mfumu, atuluke mau achifumu pakamwa pake, nalembedwe m'malamulo a Apersiya ndi Amediya, angasinthike, kuti Vasiti asalowenso pamaso pa mfumu Ahasuwero; ndi mfumu aninkhe chifumu chake kwa mnzake womposa iye. Ndipo mau amene adzaika mfumu akamveka m'ufumu wake wonse, (pakuti ndiwo waukulu), akazi onse adzachitira amuna ao ulemu, akulu ndi ang'ono. Ndipo mauwo anakonda mfumu ndi akalonga; ndi mfumu inachita monga mwa mau a Memukana, natumiza akalata kumaiko onse a mfumu, kudziko lililonse monga mwa chilembedwe chao, ndi kumtundu uliwonse monga mwa chinenedwe chao, kuti mwamuna aliyense akhale wamkulu m'nyumba yakeyake, nawabukitse monga mwa chinenedwe cha anthu a mtundu wake. Zitatha izi, utaleka mkwiyo wa mfumu Ahasuwero, anakumbukira Vasiti, ndi chochita iye, ndi chomlamulidwira. Pamenepo anyamata a mfumu omtumikira anati, Amfunire mfumu anamwali okongola; ndi mfumu aike oyang'anira m'maiko onse a ufumu wake, kuti asonkhanitse anamwali onse okongola m'chinyumba cha ku Susa, m'nyumba ya akazi; awasunge Hegai mdindo wa mfumu wosungira akazi, nawapatse zowayeretsa; ndi namwali womkonda mfumu akhale mkazi wamkulu m'malo mwa Vasiti. Ndipo chinthuchi chinamkonda mfumu, nachita chomwecho. Panali Myuda m'chinyumba cha ku Susa, dzina lake ndiye Mordekai, mwana wa Yairi, mwana wa Simei, mwana wa Kisi Mbenjamini; uyu anatengedwa ndende ku Yerusalemu, pamodzi ndi andende anatengedwa pamodzi ndi Yekoniya mfumu ya Yuda, amene Nebukadinezara mfumu ya Babiloni adamtenga ndende. Ndipo iye adalera Hadasa, ndiye Estere, mwana wamkazi wa atate wake wamng'ono; popeza iye analibe atate kapena amai; ndi namwaliyo anali wa maonekedwe okoma, ndi wokongola; ndipo atamwalira atate wake ndi mai wake, Mordekai anamtenga akhale mwana wake. Ndipo kunali, atamveka mau a mfumu ndi lamulo lake, ndipo atasonkhanidwa anamwali ambiri m'chinyumba cha ku Susa, awasunge Hegai, anamtenga Estere yemwe, alowe m'nyumba ya mfumu, amsunge Hegai wosunga akazi. Ndipo namwaliyo anamkomera, namchitira chifundo; ndipo anafulumira kumpatsa zake zomyeretsa, ndi magawo ake, ndi anamwali asanu ndi awiri oyenera kumpatsa ochokera m'nyumba ya mfumu; ndipo anamsuntha iye ndi anamwali ake akhale m'malo okometsetsa m'nyumba ya akazi. Estere sadawulula mtundu wake ndi chibale chake; pakuti Mordekai adamuuzitsa kuti asadziwulule. Ndi Mordekai akayendayenda tsiku ndi tsiku kubwalo la nyumba ya akazi, kuti adziwe umo akhalira Estere, ndi chimene chidzamchitikira. Kunafika tsono kulowa kwake kwa namwali aliyense, kuti alowe kwa mfumu Ahasuwero, atamchitira monga mwa lamulo la akazi, miyezi khumi ndi iwiri; pakuti ankakwaniritsa masiku a mayeretsedwe ao motero, miyezi isanu ndi umodzi ndi mafuta a mure, ndi miyezi isanu ndi umodzi ndi zonunkhira bwino, ndi zoyeretsa akazi. Ndipo namwali aliyense analowa kwa mfumu motero, zilizonse anafuna anampatsa zochokera m'nyumba ya akazi, alowe nazo kunyumba ya mfumu. Madzulo ake analowamo, nabwera m'mawa mwake kunka kunyumba yachiwiri ya akazi, amsunge Saasigazi mdindo wa mfumu, wosunga akazi aang'ono a mfumu; iyeyu sanalowenso kwa mfumu, koma akakondwera naye mfumu, ndi kumuitana kumtchula dzina lake, ndiko. Pofika tsono kulowa kwake kwa Estere mwana wa Abihaili, atate wamng'ono wa Mordekai, amene adadzitengera akhale mwana wake, kuti alowe kwa mfumu, sanafune kanthu koma zonena Hegai mdindo wa mfumu wosunga akazi ndizo. Ndipo Estere anayamikizidwa pamaso pa onse ompenya. Momwemo anatengedwa Estere kunka kwa mfumu Ahasuwero, kunyumba yake yachifumu, mwezi wakhumi, ndiwo mwezi wa Tebeti, chaka chachisanu ndi chiwiri cha ufumu wake. Ndipo mfumu inakonda Estere koposa akazi onse, nalandira iye kuyanja ndi chifundo pamaso pake, koposa anamwali onse; motero anaika korona wachifumu pamutu pake, namuyesa mkazi wamkulu m'malo mwa Vasiti. Pamenepo mfumu inawakonzera madyerero akulu ake onse, ndi omtumikira, ndiwo madyerero a Estere; napumulitsa maiko, naninkha zaufulu monga mwa ufulu wa mfumu. Ndipo posonkhanidwa anamwali nthawi yachiwiri Mordekai anali wa m'bwalo la mfumu. Estere sadawulula chibale chake kapena mtundu wake, monga Mordekai adamuuza; popeza Estere anachita mau a Mordekai monga m'mene analeredwa naye. Masiku awa pokhala Mordekai wa m'bwalo la mfumu, Bigitana ndi Teresi, adindo awiri a mfumu osunga pakhomo, anapsa mtima, nayesa kumthira manja mfumu Ahasuwero. Koma chidadziwika ichi kwa Mordekai, ndiye anafotokozera Estere mkazi wamkulu; ndi Estere anamuuza mfumu, kumnenera Mordekai. Ndipo atafunsira mlanduwo, anaupeza momwemo, napachikidwa onse awiri pamtengo; ndipo anachilemba m'buku la mbiri pamaso pa mfumu. Zitatha izi, mfumu Ahasuwero anamkuza Hamani mwana wa Hamedata, wa ku Agagi, namkweza, naika mpando wake upose akalonga onse okhala naye. Ndipo anyamata onse a mfumu okhala m'chipata cha mfumu anamweramira, namgwadira Hamani; pakuti mfumu idalamulira chotero za iye. Koma Mordekai sanamweramire kapena kumgwadira. Ndipo anyamata a mfumu okhala m'chipata cha mfumu anati kwa Mordekai, Ulakwiranji pa lamulo la mfumu? Kunali tsono, pomalankhula naye tsiku ndi tsiku, osawamvera iye, anauza Hamani, kuona ngati mlandu wa Mordekai udzakoma; popeza iye adawauza kuti ali Myuda. Ndipo Hamani, pakuona kuti Mordekai sanamweramire kapena kumgwadira, mtima wake unadzala mkwiyo. Koma anachiyesa chopepuka kumthira manja Mordekai yekha; pakuti adamfotokozera mtundu wake wa Mordekai; potero Hamani anafuna kuononga Ayuda onse okhala m'ufumu wonse wa Ahasuwero, ndiwo a mtundu wa Mordekai. Mwezi woyamba ndiwo mwezi wa Nisani, chaka chakhumi ndi chiwiri cha mfumu Ahasuwero, anaombeza Puri, ndiwo ula, pamaso pa Hamani tsiku ndi tsiku, mwezi ndi mwezi, mpaka mwezi wakhumi ndi chiwiri, ndiwo mwezi wa Adara. Ndipo Hamani anati kwa mfumu Ahasuwero, Pali mtundu wina wa anthu obalalika ndi ogawanikana mwa mitundu ya anthu m'maiko onse a ufumu wanu, ndi malamulo ao asiyana nao a anthu onse, ndipo sasunga malamulo a mfumu; chifukwa chake mfumu siiyenera kuwaleka. Chikakomera mfumu, chilembedwe kuti aonongeke iwo; ndipo ndidzapereka matalente a siliva zikwi khumi m'manja a iwo akusunga ntchito ya mfumu, abwere nao kuwaika m'nyumba za chuma cha mfumu. Ndipo mfumu inavula mphete yake pa chala chake, naipereka kwa Hamani mwana wa Hamedata wa ku Agagi, mdani wa Ayuda. Ndipo mfumu idati kwa Hamani, siliva akhale wako, ndi anthu omwe; uchite nao monga momwe chikukomera. Pamenepo anaitana alembi a mfumu mwezi woyamba, tsiku lake lakhumi ndi chitatu, nalembera monga mwa zonse Hamani analamulira akazembe ndi ziwanga zoyang'anira maiko ali onse, ndi akalonga a mitundu iliyonse ya anthu, maiko ali onse monga mwa chilembedwe chao, ndi mitundu iliyonse ya anthu monga mwa chinenedwe chao; anazilemba m'dzina la mfumu Ahasuwero, nazisindikiza ndi mphete ya mfumu. Ndipo anatumiza akalata ndi amtokoma kumaiko onse a mfumu, kuti aononge, aphe, napulule Ayuda onse, ndiwo ana, ndi okalamba, makanda, ndi akazi, tsiku limodzi, ndilo tsiku lakhumi ndi chitatu la mwezi wakhumi ndi chiwiri, ndiwo mwezi wa Adara; nalande zao mofunkha. Mau a cholembedwacho, ndiwo kuti lichitike lamulo m'maiko onse, analalikidwa kwa anthu onse, kuti akonzekeretu tsiku lomwelo. Amtokoma anatuluka ofulumizidwa ndi mau a mfumu, ndi lamulo linabukitsidwa m'chinyumba cha ku Susa; ndipo mfumu ndi Hamani anakhala pansi kumwa; koma mudzi wa Susa unadodoma. Koma podziwa Mordekai zonse zidachitikazi, Mordekai anang'amba zovala zake, navala chiguduli ndi mapulusa, natuluka pakati pa mudzi, nafuula, nalira kulira kwakukulu ndi kowawa, nafika popenyana ndi chipata cha mfumu; popeza sanathe munthu kulowa kuchipata cha mfumu wovala chiguduli. Ndi m'maiko monse, paliponse anafikapo mau a mfumu ndi lamulo lake, panali maliro akulu mwa Ayuda, ndi kusala, ndi kulira misozi, ndi kubuma; nagona m'chiguduli ndi mapulusa ambiri. Ndipo anamwali a Estere ndi adindo ake anadza, namuuza; ndi mkazi wamkulu anawawidwa mtima kwambiri, natumiza chovala aveke Mordekai, ndi kumchotsera chiguduli chake; koma sanachilandira. Pamenepo Estere anaitana Hataki mdindo wina wa mfumu, amene idamuika amtumikire, namuuza amuke kwa Mordekai, kuti adziwe ichi nchiyani ndi chifukwa chake ninji. Natuluka Hataki kunka kwa Mordekai kukhwalala la mudzi linali popenyana ndi chipata cha mfumu. Ndipo Mordekai anamfotokozera zonse zidamgwera, ndi mtengo wake wa ndalama adati Hamani adzapereka m'nyumba ya chuma cha mfumu pa Ayuda, kuwaononga. Anampatsanso chitsanzo cha lamulo lolembedwa adalibukitsa m'Susa, kuwaononga, achionetse kwa Estere, ndi kumfotokozera, ndi kumlangiza alowe kwa mfumu, kumpembedza, ndi kupempherera anthu ake kwa iye. Nadza Hataki, namuuza Estere mau a Mordekai. Pamenepo Estere ananena ndi Hataki, namtuma akauze Mordekai, ndi kuti, Akapolo onse a mfumu ndi anthu a m'maiko a mfumu adziwa kuti aliyense, ngakhale wamwamuna kapena wamkazi, akalowa kwa mfumu kubwalo la m'katimo wosaitanidwa, lamulo la pa iye ndi limodzi, ndilo kuti amuphe, akapanda mfumu kumloza ndi ndodo yachifumu yagolide kuti akhale ndi moyo; koma ine sanandiitane ndilowe kwa mfumu masiku awa makumi atatu. Ndipo anamuuza Mordekai mau a Estere. Koma Mordekai anawauza ambwezere mau Estere, kuti, Usamayesa m'mtima mwako kuti udzapulumuka m'nyumba ya mfumu koposa Ayuda onse ena. Pakuti ukakhala chete konse tsopano lino, chithandizo ndi chipulumutso kwa Ayuda zidzafuma kwina; koma iwe ndi nyumba ya atate wako mudzaonongeka; ndipo kaya, kapena walowera ufumu chifukwa cha nyengo yonga iyi. Pamenepo Estere anati ambwezere mau Mordekai, Muka, sonkhanitsa Ayuda onse opezeka m'Susa, nimundisalire, osadya osamwa masiku atatu, usiku ndi usana, ine ndemwe ndi anamwali anga tidzasala momwemo, ndipo motero ndidzalowa kwa mfumu, ndiko kosalingana ndi lamulo; ndikaonongeka tsono ndionongeke. Napita Mordekai, nachita monga mwa zonse adamlamulira Estere. Ndipo kunali tsiku lachitatu, Estere anavala zovala zake zachifumu, nakaimirira m'bwalo la m'kati la nyumba ya mfumu, popenyana pa nyumba ya mfumu; ndi mfumu inakhala pa mpando wake wachifumu m'nyumba yachifumu, pandunji polowera m'nyumba. Ndipo kunali, pamene mfumu inaona Estere mkazi wamkuluyo alikuima m'bwalo, inamkomera mtima; ndi mfumu inamloza Estere ndi ndodo yachifumu yagolide inali m'dzanja lake. Nayandikira Estere, nakhudza nsonga ya ndodoyo. Ninena naye mfumu, Mufunanji, Estere mkazi wamkulu? Pempho lanu nchiyani? Lidzaperekedwa kwa inu, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumuwo. Ndipo Estere anati, Chikakomera mfumu, adze mfumu ndi Hamani lero ku madyerero ndinawakonzera. Niti mfumu, Mumfulumize Hamani, achitike mau a Estere. Nidza mfumu ndi Hamani ku madyerero adawakonzera Estere. Ndipo mfumu inati kwa Estere pa madyerero a vinyo, Pempho lanu nchiyani? Lidzaperekedwa kwa inu; mufunanji? Chidzachitika, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumuwo. Nayankha Estere, nati, Pempho langa ndi kufuna kwanga ndiko, ngati mfumu indikomera mtima, ngatinso chakomera mfumu kupereka pempho langa ndi kuchita chofuna ine, adze mfumu ndi Hamani ku madyerero ndidzawakonzera; ndipo mawa ndidzachita monga yanena mfumu. Ndipo Hamani anatuluka tsiku lomwelo wosekerera ndi wokondwera mtima; koma pamene Hamani anapenya Mordekai kuchipata cha mfumu, osamnyamukira kapena kumfumukira, Hamani anadzazidwa ndi mkwiyo pa Mordekai. Koma Hamani anadziletsa, namuka kwao, natumiza munthu kukatenga mabwenzi ake, ndi Zeresi mkazi wake. Nawawerengera Hamani kulemera kwake kwakukulu, ndi ana ake ochuluka, ndi zonse mfumu idamkuza nazo, ndi umo adamkweza koposa akalonga ndi anyamata a mfumu. Hamani anatinso, Ndiponso Estere mkazi wamkulu sanalole mmodzi yense alowe pamodzi ndi mfumu ku madyerero adakonzawo, koma ine ndekha; nandiitana mawanso pamodzi ndi mfumu. Koma zonsezi sindipindula nazo kanthu konse, pokhala ndilikuona Mordekai Myudayo alikukhala kuchipata cha mfumu. Pamenepo Zeresi mkazi wake, ndi mabwenzi ake onse ananena naye, Apange mtengo, msinkhu wake mikono makumi asanu, ndi mawa mukanene nayo mfumu kuti ampachike Mordekai pamenepo; nimulowe pamodzi ndi mfumu kumadyerero wokondwera. Ndipo ichi chidakomera Hamani, napangitsa anthu mtengowo. Usiku uja tulo tidamwazikira mfumu, niti abwere nalo buku la mbiri, naliwerenga pamaso pa mfumu. Napeza mudalembedwa kuti Mordekai adawulula za Bigitana ndi Teresi, awiri a adindo a mfumu osunga pakhomo, amene adayesa kumthira manja mfumu Ahasuwero. Niti mfumu, Anamchitira Mordekai ulemu ndi ukulu wotani chifukwa cha ichi? Ndipo anyamata a mfumu akuitumikira ananena nayo, Sanamchitire kanthu. Niti mfumu, Ali kubwalo ndani? Koma Hamani adalowa m'bwalo lakunja la nyumba ya mfumu kulankhula ndi mfumu za kupachika Mordekai pamtengo adaukonzeratu. Ndipo anyamata a mfumu ananena nayo, Taonani, Hamani alikuima pabwalo. Niti mfumu, Alowe. Nalowa Hamani. Ndipo mfumu inati kwa iye, Kodi amchitire chiyani munthu amene mfumu ikondwera kumchitira ulemu? Ndipo Hamani anati mumtima mwake, Ndaniyo mfumu ikondwera kumchitira ulemu koposa ine? Nati Hamani kwa mfumu, Munthu amene mfumu ikondwera kumchitira ulemu, amtengere chovala chachifumu amachivala mfumu, ndi kavalo amakwerapo mfumu, naike korona wachifumu pamutu pake, napereke chovala ndi kavalo m'dzanja la wina womveketsa wa akalonga a mfumu, naveke nacho munthu amene mfumu ikondwera kumchitira ulemu, namuyendetse pa kavaloyo m'khwalala la m'mudzi, nafuule pamaso pake, Azitero naye munthu amene mfumu ikondwera kumchitira ulemu. Pamenepo mfumu inati kwa Hamani, Fulumira, tenga chovala ndi kavalo monga umo wanenera, nuchitire chotero Mordekai Myudayo, wokhala pa chipata cha mfumu; kasasowepo kanthu ka zonse wazinena. Ndipo Hamani anatenga chovala ndi kavalo, naveka Mordekai, namuyendetsa pa kavalo m'khwalala la m'mudzi, nafuula pamaso pake, Azitero naye munthu amene mfumu ikondwera kumchitira ulemu. Ndipo Mordekai anabweranso kuchipata cha mfumu. Koma Hamani anafulumira kunka kwao, wachisoni ndi wofunda mutu wake. Ndipo Hamani anafotokozera Zeresi mkazi wake, ndi mabwenzi ake onse, zonse zidamgwera. Nanena naye anzeru ake, ndi Zeresi mkazi wake, Mordekai amene wayamba kutsika pamaso pake, akakhala wa mbumba ya Ayuda, sudzamlaka; koma udzagwada pamaso pake. Akali chilankhulire naye, anafika adindo a mfumu, nafulumira kumtenga Hamani kunka naye kumadyerero adawakonzera Estere. Motero inadza mfumu ndi Hamani kumwa naye mkazi wamkulu Estere. Nitinso mfumu kwa Estere tsiku lachiwirili pa madyerero a vinyo, Pempho lanu nchiyani, mkazi wamkulu Estere? Lidzapatsidwa kwa inu; mufunanji? Chidzachitika, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumu wanga. Nayankha mkazi wamkulu Estere, nati, Ngati mwandikomera mtima, mfumu, ndipo chikakomera mfumu, andilekere moyo wanga pa kupempha kwanga, ndi wa anthu a mtundu wanga pa pempho langa; pakuti tagulitsidwa; ine ndi anthu a mtundu wanga, kuti ationonge, atiphe, natipulule. Koma tikadagulitsidwa tikhale akapolo ndi adzakazi, ndikadakhala chete; chinkana wosautsa sakadakhoza kubwezera kusowa kwa mfumu. Pamenepo mfumu Ahasuwero inalankhula, niti kwa mkazi wamkulu Estere, Ndani uyu, ali kuti iyeyu wadzazidwa mtima wake kuti azitero? Nati Estere, Munthu wosautsa ndi mdani ndiye Hamani woipa uyu. Pamenepo Hamani anagwidwa mantha pamaso pa mfumu ndi mkazi wamkulu. Ninyamuka mfumu mu mkwiyo wake ku madyerero a vinyo, nimka kumunda wa maluwa wa kuchinyumba; koma Hamani anatsalira kudzipempherera moyo kwa mkazi wamkulu Estere; popeza anapenya kuti mfumu inatsimikiza mtima kumchitira choipa. Nibwera mfumu kumunda wa maluwa wa kuchinyumba kulowanso m'nyumba munali madyerero a vinyo, napeza Hamani atagwa pa kama wokhalapo Estere. Niti mfumu, Kodi aumiriza mkazi wamkulu pamaso panga m'nyumba? Potuluka mau pakamwa pa mfumu anamphimba Hamani nkhope. Nati Haribona wina wa adindo okhala pamaso pa mfumu, Taonaninso, mtengowo msinkhu wake mikono makumi asanu, umene Hamani anaupangira Mordekai wonenera mfumu zokoma, uimiritsidwa m'nyumba ya Hamani. Niti mfumu, Mpachike pomwepo. Nampachika Hamani pa mtengo adaukonzera Mordekai. Pamenepo mkwiyo wa mfumu unatsika. Tsiku lomwelo mfumu Ahasuwero anampatsa mkazi wamkulu Estere nyumba ya Hamani mdani wa Ayuda. Nafika Mordekai pamaso pa mfumu; pakuti Estere adamuuza za chibale chake. Ndipo mfumu inavula mphete yake adailanda kwa Hamani, naipereka kwa Mordekai. Ndi Estere anaika Mordekai akhale woyang'anira nyumba ya Hamani. Nanenanso Estere pamaso pa mfumu, nagwa ku mapazi ake, nalira misozi, nampembedza kuti achotse choipacho cha Hamani wa ku Agagi, ndi chiwembu adachipangira Ayuda. Ndipo mfumu inaloza Estere ndi ndodo yachifumu yagolide. Nanyamuka Estere, naima pamaso pa mfumu. Nati, Chikakomera mfumu, ndipo ngati yandikomera mtima, nichiyenera kwa mfumu, ngatinso ndimchititsa kaso, alembere chosintha mau a akalata a chiwembu cha Hamani mwana wa Hamedata wa ku Agagi, amene adawalembera kuononga Ayuda okhala m'maiko onse a mfumu; pakuti ndidzapirira bwanji pakuchiona choipa chilikudzera a mtundu wanga, kapena ndidzapirira bwanji pakuchiona chionongeko cha fuko langa? Pamenepo mfumu Ahasuwero anati kwa mkazi wamkulu Estere, ndi kwa Mordekai Myuda, Taonani, ndampatsa Estere nyumba ya Hamani, ndi iyeyu anampachika pamtanda, chifukwa anatulutsa dzanja lake pa Ayuda. Mulembere inunso kwa Ayuda monga mufuna, m'dzina la mfumu, nimusindikize ndi mphete ya mfumu; pakuti kalata wolembedwa m'dzina la mfumu, ndi kusindikizika ndi mphete ya mfumu, palibe munthu akhoza kumsintha. Pamenepo anaitana alembi a mfumu nthawi yomweyo, mwezi wachitatu, ndiwo mwezi wa Sivani, tsiku lake la makumi awiri ndi chitatu, monga mwa zonse Mordekai analamulira; nalembera kwa Ayuda, ndi kwa akazembe, ndi ziwanga, ndi akalonga a kumaiko, oyambira ku Indiya, ofikira ku Kusi, maiko zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi awiri, ku dziko lililonse monga mwa chilembedwe chao, ndi mtundu uliwonse monga mwa chinenedwe chao, ndi kwa Ayuda monga mwa chinenedwe chao. Ndipo analembera m'dzina la mfumu Ahasuwero, nasindikiza ndi mphete ya mfumu, natumiza akalata ndi amtokoma pa akavalo, okwera pa akavalo aliwiro achifumu, obadwa mosankhika; m'menemo mfumu inalola Ayuda okhala m'midzi iliyonse asonkhane, ndi kulimbikira moyo wao, kuononga, kupha, ndi kupulula mphamvu yonse ya anthu ndi ya dziko yofuna kuwathira nkhondo, iwo, ana ang'ono ao, ndi akazi ao, ndi kulanda zofunkha zao, tsiku lomwelo, m'maiko onse a mfumu Ahasuwero, tsiku lakhumi ndi chitatu la mwezi wakhumi ndi chiwiri, ndiwo mwezi wa Adara. Chitsanzo chake, cha lemboli, chakuti abukitse lamulo m'maiko onse, chinalalikidwa kwa mitundu yonse ya anthu, kuti, Ayuda akonzekeretu tsiku lijalo, kubwezera chilango adani ao. Natuluka amtokoma okwera pa akavalo aliwiro achifumu; pakuti mau a mfumu anawafulumiza ndi kuwaumiriza; ndipo lamulolo linabukitsidwa m'chinyumba cha ku Susa. Ndipo Mordekai anatuluka pamaso pa mfumu wovala chovala chachifumu chamadzi ndi choyera, ndi korona wamkulu wagolide, ndi malaya abafuta ndi ofiirira; ndi mudzi wa Susa unafuula ndi kukondwera. Ayuda anali nako kuunika, ndi kukondwera, ndi chimwemwe, ndi ulemu. Ndi m'maiko monse, ndi m'midzi yonse, mudafika mau a mfumu ndi lamulo lake, Ayuda anali nako kukondwera ndi chimwemwe, madyerero ndi tsiku lokoma. Ndipo ambiri a mitundu ya anthu a m'dziko anasanduka Ayuda; pakuti kuopsa kwa Ayuda kudawagwera. Mwezi wakhumi ndi chiwiri tsono, ndiwo mwezi wa Adara, tsiku lake lakhumi ndi chitatu, mau a mfumu ndi lamulo lake ali pafupi kuchitika, tsikuli adani a Ayuda anayesa kuwachitira ufumu, koma chinasinthika; popeza Ayuda anachitira ufumu iwo odana nao; pakuti Ayuda anasonkhana pamodzi m'midzi mwao, m'maiko onse a mfumu Ahasuwero, kuwathira manja ofuna kuwachitira choipa, ndipo palibe munthu analimbika pamaso pao; popeza kuopsa kwao kudawagwera mitundu yonse ya anthu. Ndipo akalonga onse a maikowo, ndi akazembe, ndi ziwanga, ndi iwo ochita ntchito ya mfumu, anathandiza Ayuda; popeza kuopsa kwa Mordekai kudawagwera. Pakuti Mordekai anali wamkulu m'nyumba ya mfumu, ndi mbiri yake idabuka m'maiko onse; pakuti munthuyu Mordekai anakulakulabe. Ndipo Ayuda anakantha adani ao onse, kuwakantha ndi lupanga, ndi kuwapulula, nachitira odana nao monga anafuna. Ndipo m'chinyumba cha ku Susa Ayuda anakantha, naononga amuna mazana asanu. Napha Parasadata, ndi Dalifoni, ndi Asipata, ndi Porata, ndi Adaliya, ndi Aridata, ndi Parimasta, ndi Arisai, ndi Aridai, ndi Vaizata, ana amuna khumi a Hamani mwana wa Hamedata, mdani wa Ayuda. Koma sanalande zofunkha. Tsiku lomwelo anabwera nacho kwa mfumu chiwerengo cha iwo ophedwa m'chinyumba cha ku Susa. Ndipo mfumu inati kwa mkazi wamkulu Estere, Ayuda adapha, naononga amuna mazana asanu m'chinyumba cha ku Susa, ndi ana amuna khumi a Hamani; nanga m'maiko ena a mfumu munachitikanji? Pempho lanu ndi chiyani tsono? Lidzachitikira inu; kapena mufunanjinso? Kudzachitika. Nati Estere, Chikakomera mfumu, alole Ayuda okhala m'Susa achite ndi mawa lomwe monga mwa lamulo la lero; ndi ana amuna khumi a Hamani apachikidwe pamtengo. Ndipo mfumu inati azichita motero, nalamulira m'Susa, napachikidwa ana amuna khumi a Hamani. Ndipo Ayuda okhala m'Susa anasonkhana pamodzi, tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi wa Adara, napha amuna mazana atatu m'Susa; koma sanalande zofunkha. Nasonkhana pamodzi Ayuda ena okhala m'maiko a mfumu, nalimbikira moyo wao, napumula pa adani ao, nawapha a iwo odana nao zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu; koma sanalande zofunkha. Chinachitika ichi tsiku lakhumi ndi chitatu la mwezi wa Adara, ndi tsiku lake lakhumi ndi chinai anapumula, naliyesa tsiku lamadyerero ndi lakukondwera. Koma Ayuda okhala m'Susa anasonkhana tsiku lakhumi ndi chitatu ndi lakhumi ndi chinai, ndi pa tsiku lakhumi ndi chisanu anapumula, naliyesa tsiku lamadyerero ndi lakukondwera. Chifukwa chake Ayuda a kumilaga, okhala m'midzi yopanda malinga, amaliyesa tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi wa Adara tsiku la kukondwera ndi madyerero, ndi tsiku lokoma, ndi lakutumizirana magawo. Ndipo Mordekai analembera izi, natumiza akalata kwa Ayuda onse okhala m'maiko onse a mfumu Ahasuwero, a kufupi ndi a kutali, kuwalimbikitsira, asunge tsiku lakhumi ndi chinai, mwezi wa Adara, ndi tsiku lake lakhumi ndi chisanu lomwe, chaka ndi chaka, ndiwo masiku amene Ayuda anapumula pa adani ao; ndi mwezi wachisoni unawasandulikira wakukondwera, ndi wamaliro ukhale tsiku lokoma, awayese masiku amadyerero ndi akukondwera, akutumizirana magawo, ndi akupatsa zaufulu kwa osauka. Ndipo Ayuda anavomereza kuchita monga umo adayambira, ndi umo Mordekai adawalembera; popeza Hamani mwana wa Hamedata wa ku Agagi, mdani wa Ayuda onse, adapangira Ayuda chiwembu kuwaononga, naombeza Puri, ndiwo ula, kuwatha ndi kuwaononga; koma pofika mlanduwo kwa mfumu, anati mwa akalata kuti chiwembu chake choipa adachipangira Ayuda, chimbwerere mwini; ndi kuti iye ndi ana amuna ake apachikidwe pamtengo. Chifukwa chake anatcha masikuwa Purimu, ndilo dzina la ulawo. Momwemo, chifukwa cha mau onse a kalatayo, ndi izi adaziona za mlanduwo, ndi ichi chidawadzera, Ayuda anakhazikitsa ichi, nadzilonjezetsa okha, ndi mbeu yao, ndi onse akuphatikana nao, chingalekeke, kuti adzasunga masiku awa awiri monga mwalembedwa, ndi monga mwa nyengo yao yoikika, chaka ndi chaka; ndi kuti masikuwa adzakumbukika ndi kusungika mwa mibadwo yonse, banja lililonse, dziko lililonse, ndi mudzi uliwonse; ndi kuti masiku awa sadzalekeka mwa Ayuda, kapena kusiyidwa chikumbukiro chao mwa mbeu yao. Pamenepo Estere mkazi wamkulu mwana wa Abihaili, ndi Mordekai Myuda, analembera molamulira, kukhazikitsa kalata uyu wachiwiri wa Purimu. Natumiza iye akalata kwa Ayuda onse, kumaiko zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi awiri a ufumu wa Ahasuwero, ndiwo mau a mtendere ndi choonadi; kukhazikitsa masiku awa a Purimu m'nyengo zao, m'mene Mordekai Myuda ndi mkazi wamkulu Estere adawakhazikitsira; ndi umo anadzikhazikitsira okha, ndi mbeu yao, kunena za kusala kwao, ndi kufuula kwao. Ndipo kunena kwake kwa Estere kunakhazikitsa mau awa a Purimu; ndipo kunalembedwa m'buku. Ndipo mfumu Ahasuwero inasonkhetsa dziko, ndi zisumbu za ku nyanja. Ndi zochita zonse za mphamvu yake, ndi nyonga zake, ndi mafotokozedwe a ukulu wa Mordekai, umene mfumu inamkulitsa nao, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Mediya ndi Persiya? Pakuti Mordekai Myuda anatsatana naye mfumu Ahasuwero, nakhala wamkulu mwa Ayuda, navomerezeka mwa unyinji wa abale ake wakufunira a mtundu wake zokoma, ndi wakunena za mtendere kwa mbeu yake yonse. Panali munthu m'dziko la Uzi, dzina lake ndiye Yobu; ndipo munthuyu anali wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa. Ndipo anabala ana amuna asanu ndi awiri, ndi ana akazi atatu. Zoweta zakenso zinali nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi ngamira zikwi zitatu, ndi ng'ombe zamagoli mazana asanu, ndi abulu akazi mazana asanu, antchito ake omwe ndi ambiri; chotero munthuyu anaposa anthu onse a kum'mawa. Ndipo ana ake amuna anamuka kukachita madyerero m'nyumba ya yense pa tsiku lake; natumiza mthenga kuitana alongo ao atatu adzadye nadzamwe nao. Ndipo kunatero, atatha masiku a madyererowa Yobu anatumiza mau, nawapatula, nauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, monga mwa kuwerenga kwa iwo onse; pakuti Yobu anati, Kapena anachimwa ana anga, nachitira Mulungu mwano m'mtima mwao, Anatero Yobu masiku onse. Ndipo panali tsiku lakuti ana a Mulungu anadza kudzionetsa kwa Yehova, nadzanso Satana pakati pao. Nati Yehova kwa Satana, Ufuma kuti? Nayankha Satana kwa Yehova, nati, Kupitapita m'dziko ndi kuyendayenda m'mwemo. Ndipo Yehova anati kwa Satana, Kodi waonerera mtumiki wanga Yobu? Pakuti palibe wina wonga iye m'dzikomo, munthu wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa. Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Kodi Yobu aopa Mulungu pachabe? Kodi simunamtchinga iye ndi nyumba yake, ndi zake zonse, pomzinga ponse? Ntchito ya manja ake mwaidalitsa, ndi zoweta zake zachuluka m'dziko. Koma mutambasule dzanja lanu ndi kumkhudzira zake zonse, ndipo adzakuchitirani mwano pamaso panu. Nati Yehova kwa Satana, Taona, zonse ali nazo zikhale m'dzanja mwako; pa iye pokha usatambasula dzanja lako. Natuluka Satana pamaso pa Yehova. Tsono panali tsiku loti ana ake aamuna ndi aakazi analinkudya ndi kumwa vinyo m'nyumba ya mkulu wao; nafika mthenga kwa Yobu, nati, Ng'ombe zinalikulima, ndi abulu akazi analikudya pambali pao; koma anazigwera Aseba, nazitenga, nawapha anyamata ndi lupanga lakuthwa, ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani. Akali chilankhulire uyu, anadza winanso, nati, Wagwa moto wa Mulungu wochokera kumwamba, wapsereza nkhosa ndi anyamata, nuzinyeketsa; ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani. Akali chilankhulire uyu, anadza winanso, nati, Ababiloni anadzigawa magulu atatu, nazigwera ngamira, nazitenga, nawapha anyamata ndi lupanga lakuthwa, ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani. Akali chilankhulire, anadza winanso, nati, Ana anu aamuna ndi aakazi analinkudya ndi kumwa vinyo m'nyumba ya mkulu wao; ndipo taonani, inadza mphepo yaikulu yochokera kuchipululu, niomba pangodya zonse zinai za nyumbayo, nigwa pa anyamatawo, nafa; ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani. Pamenepo Yobu ananyamuka, nang'amba malaya ake, nameta mutu wake, nagwa pansi, nalambira, nati, Ndinatuluka m'mimba ya mai wanga wamaliseche, wamaliseche ndidzamukanso; Yehova anapatsa, Yehova watenga, lidalitsike dzina la Yehova. Mwa ichi chonse Yobu sanachimwe, kapena kunenera Mulungu cholakwa. Panalinso tsiku lakuti anadza ana a Mulungu kudzionetsa kwa Yehova, nadza Satana yemwe pakati pao kudzionetsa kwa Yehova. Ndipo Yehova anati kwa Satana, Ufuma kuti? Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Kupitapita m'dziko, ndi kuyendayenda m'mwemo. Ndipo Yehova anati kwa Satana, Kodi waonerera mtumiki wanga Yobu? Pakuti palibe wina wonga iye m'dzikomo, munthu wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu, ndi kupewa zoipa; naumirirabe kukhala wangwiro, chinkana undisonkhezera ndimuononge kopanda chifukwa. Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Khungu kulipa khungu, inde munthu adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo wake. Koma tambasulani dzanja lanu, ndi kukhudza fupa lake ndi mnofu wake, ndipo adzakuchitirani mwano pamaso panu. Ndipo Yehova anati kwa Satana, Taona, akhale m'dzanja lako; moyo wake wokha uuleke. Natuluka Satana pamaso pa Yehova, nazunza Yobu ndi zilonda zowawa, kuyambira kuphazi lake kufikira pakati pamutu pake. Ndipo anadzitengera phale, kudzikanda nalo; nakhala pansi m'maphulusa. Pamenepo mkazi wake ananena naye, Kodi uumiriranso kukhala wangwiro? Chitira Mulungu mwano, ufe. Koma ananena naye, Ulankhula monga amalankhula akazi opusa. Ha! Tidzalandira zokoma kwa Mulungu kodi, osalandiranso zoipa? Pa ichi chonse Yobu sanachimwe ndi milomo yake. Atamva tsono mabwenzi atatu a Yobu za choipa ichi chonse chidamgwera, anadza, yense kuchokera kwao, Elifazi wa ku Temani, ndi Bilidadi Msuki, ndi Zofari wa ku Naama, napangana kudzafika kumlirira ndi kumsangalatsa. Ndipo pokweza maso ao ali kutali, sanamdziwe, nakweza mau ao, nalira; nang'amba yense malaya ake, nawaza fumbi kumwamba ligwe pamitu pao. Nakhala pansi pamodzi naye panthaka masiku asanu ndi awiri usana ndi usiku, palibe mmodzi ananena naye kanthu, popeza anaona kuti kuwawaku nkwakukulu ndithu. Atatero, Yobu anatsegula pakamwa pake, natemberera tsiku lake. Nalankhula Yobu nati, Litayike tsiku lobadwa ine, ndi usikuwo udati, Waima naye mwana wamwamuna. Tsiku lija likhale mdima; Mulungu asalifunse kumwamba, ndi kuunika kusaliwalire. Mdima ndi mthunzi wa imfa ziliyese laolao; mtambo ulikhalire; zonse zodetsa usana bii ziliopse. Usiku uja, mdima weniweni uugwere; usakondwerere mwa masiku a m'chaka; usalowe m'chiwerengedwe cha miyezi. Ha! Usiku uja ukhale chumba; kuimbira kokondwera kusalowe m'mwemo. Autemberere iwo akutemberera usana, Odziwa kuutsa Leviyatani. Nyenyezi za chizirezire zide; uyembekezere kuunika, koma kuusowe; usaone kephenyuka kwa mbandakucha; popeza sunatseka pa makomo ake mimba ya mai wanga. Kapena kundibisira mavuto pamaso panga. Ndinalekeranji kufera m'mimba? Ndi kupereka mzimu wanga pobadwa ine. Anandilandiriranji maondo? Kapena mawere kuti ndiyamwe? Pakuti ndikadagona pansi pomwepo ndi kukhala chete; ndikanagona tulo; pamenepo ndikadaona popumula; pamodzi ndi mafumu ndi maphungu a padziko, akudzimangira m'mabwinja; kapena pamodzi ndi akalonga eni ake a golide, odzaza nyumba zao ndi siliva; Kapena ngati nsenye yobisika ndikadakhala kuli zii; ngati makanda osaona kuunika. Apo oipa aleka kumavuta; ndi apo ofooka mphamvu akhala m'kupumula. Apo a m'kaidi apumula pamodzi, osamva mau a wofulumiza wao. Ang'ono ndi akulu ali komwe; ndi kapolo amasuka kwa mbuyake. Amninkhiranji kuunika wovutika, ndi moyo kwa iye wakuwawa mtima, wakuyembekezera imfa, koma kuli zii, ndi kuikumba koposa chuma chobisika, wakusekerera ndi chimwemwe ndi kukondwera pakupeza manda? Amuonetseranji kuunika munthu wa njira yobisika, amene wamtsekera Mulungu? Pakuti ndikati ndidye, kumadza kuusa moyo kwanga; ndi kudzuma kwanga kumathiridwa ngati madzi. Pakuti chimene ndinachiopa chandigwera, ndi chimene ndachita nacho mantha chandidzera. Wosakhazikika, ndi wosakhala chete, ndi wosapumula ine, koma mavuto anandidzera. Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha, nati, Munthu akayesa kunena nawe mau, kodi udzamva nao chisoni? Koma akhoza ndani kudziletsa kunena? Taona iwe walangiza aunyinji, walimbitsa manja a ofooka. Mau ako anachirikiza iye amene akadagwa, walimbitsanso maondo otewa. Koma tsopano chakufikira iwe, ndipo ukomoka; chikukhudza, ndipo uvutika. Kodi kulimbika mtima kwako si ndiko kuti uopa Mulungu, ndi chiyembekezo chako si ndiwo ungwiro wa njira zako? Takumbukira tsopano, watayika ndani wosapalamula konse? Kapena oongoka mtima alikhidwa kuti? Monga umo, ndaonera, olimira mphulupulu, nabzala vuto, akololapo zomwezo. Atayika ndi mpweya wa Mulungu, nathedwa ndi mpumo wa mkwiyo wake. Kubangula kwa mkango, ndi kulira kwa mkango waukali kwaletsedwa, ndi mano a misona ya mkango athyoledwa. Mkango wokalamba udzifera posowa mkoka, ndi misona ya mkango waukazi imwazika. Anditengera mau m'tseri, m'khutu mwanga ndinalandira kunong'oneza kwake. M'malingaliro a masomphenya a usiku, powagwira anthu tulo tatikulu Anandidzera mantha ndi kunjenjemera, nanthunthumira nako mafupa anga onse. Pamenepo panapita mzimu pamaso panga; tsitsi la thupi langa lidati nyaunyau. Unaima chilili, koma sindinatha kuzindikira maonekedwe ake; panali mzukwa pamaso panga; kunali chete, ndipo ndidamva mau akuti, Kodi munthu adzakhala wolungama ndi kuposa Mulungu? Kodi munthu adzakhala woyera woposa Mlengi wake? Taona, sakhulupirira atumiki ake; nawanenera amithenga ake zopusa; kopambana kotani nanga iwo akukhala m'nyumba zadothi, amene kuzika kwao kuli m'fumbi, angothudzulidwa ngati njenjete. Kuyambira m'mawa kufikira madzulo athudzuka; aonongeka kosatha, osasamalirako munthu. Kukometsetsa kwao sikumachotsedwa nao? Amafa koma opanda nzeru. Itana tsono; pali wina wakukuyankha kodi? Ndipo udzatembenukira kwa yani wa oyera mtimawo? Pakuti mkwiyo umapha wopusa, ndi nsanje imakantha wopanda pake. Ndinapenya wopusa woyala mizu; koma pomwepo ndinatemberera pokhala pake. Ana ake akhala otekeseka, napsinjika kuchipata, wopanda wina wakuwapulumutsa. Zokolola zao anjala azidya, azitenga ngakhale kuminga, ndi aludzu ameza chuma chao. Pakuti nsautso sutuluka m'fumbi, ndi mavuto saphuka m'nthaka. Koma munthu abadwira mavuto, monga mbaliwali zikwera ziuluzika. Koma ine ndikadafuna Mulungu, ndikadaikira mlandu wanga Mulungu; amene achita zazikulu ndi zosalondoleka, zinthu zodabwitsa zosawerengeka. Amene avumbitsa mvula panthaka, natumiza madzi paminda; kuika opeputsidwa pamalo ponyamuka, kuti iwo a maliro akwezedwe kosatekeseka. Apititsa pachabe ziwembu za ochenjera, kuti manja ao sakhoza kuchita chopangana chao. Akola eni nzeru m'kuchenjera kwao, ndi uphungu wa opotoka mtima usonthokera pachabe. Iwo akomana ndi mdima pali dzuwa, nayambasa dzuwa lili pakati pamtu monga usiku. Apulumutsa aumphawi kulupanga la kukamwa kwao, ndi kudzanja la wamphamvu. Potero aumphawi ali nacho chiyembekezo, ndi mphulupulu yatsekedwa pakamwa. Taona, wodala munthu amene Mulungu amdzudzula; chifukwa chake usapeputsa kulanga kwa Wamphamvuyonse. Pakuti apweteka, namanganso mabala; alasa, ndi manja ake omwe apoletsa. Adzakupulumutsa m'masautso asanu ndi limodzi; chinkana mwa asanu ndi awiri palibe choipa chidzakukhudza. Adzakuombola kuimfa m'njala, ndi kumphamvu ya lupanga m'nkhondo. Udzabisikira mkwapulo wa lilime, sudzachiopanso chikadza chipasuko. Chipasuko ndi njala udzaziseka; ngakhale zilombo za padziko osaziopa. Pakuti udzakhala ndi pangano ndi miyala ya kuthengo; ndi nyama za kuthengo zidzakhala nawe mumtendere. Ndipo udzapeza kuti pahema pako mpa mtendere; nudzazonda za m'banja mwako osasowapo kanthu. Udzapezanso kuti mbeu zako zidzachuluka, ndi obala iwe ngati zitsamba za padziko. Udzafika kumanda utakalamba, monga abwera nao mtolo wa tirigu m'nyengo yake. Taona, ichi tachifunafuna, chili chotero; uchimvere, nuchidziwire wekha. Koma Yobu anayankha, nati, Mwenzi atayesa bwino chisoni changa, ndi kuika matsoka anga pamodzi pamuyeso! Pakuti zikadalemera tsopano koposa mchenga wa kunyanja; chifukwa chake mau anga ndasonthokera kunena. Pakuti mivi ya Wamphamvuyonse yandilowa, mzimu wanga uwumwa ulembe wake; zoopsa za Mulungu zindindandira nkhondo. Kodi mbidzi ilira pokhala nao msipu? Ilira kodi ng'ombe pa chakudya chake? Kodi chinthu chosakolera chidyeka chopanda mchere? Choyera cha dzira chikolera kodi? Zimene moyo wanga ukana kuzikhudza zikunga chakudya chosakolera kwa ine. Ha! Ndikadakhala nacho chimene ndichipempha, Mulungu akadandipatsa chimene ndichilira! Chimkomere Mulungu kundiphwanya, alole dzanja lake lindilikhe! Pamenepo ndidzasangalala, ndidzakondwera nacho chowawa chosandileka; pakuti sindinawabisa mau a Woyerayo. Mphamvu yanga njotani kuti ndiyembekeze? Mathedwe anga ndi otani kuti ndipirire? Kodi mphamvu yanga ndiyo mphamvu ya miyala? Mnofu wanga ndi mkuwa kodi? Mulibe thandizo mwa ine ndekha; chipulumutso chandithawa. Iye amene akadakomoka, bwenzi lake ayenera kumchitira chifundo; angaleke kuopa Wamphamvuyonse. Abale anga anachita monyenga ngati kamtsinje, ngati madzi a timitsinje akupitirira. Amada chifukwa cha madzi oundana. M'menemo chipale chofewa chibisika; atafikira mafundi, mitsinje iuma; kukatentha, imwerera m'malo mwao. Aulendo akutsata njira yao apatukapo, akwerera poti see, natayika. Aulendo a ku Tema anapenyerera, makamu a ku Sheba anaiyembekezera. Anazimidwa popeza adaikhulupirira; anafikako, nathedwa nzeru. Pakuti tsopano mukhala momwemo; muona choopsa, muchitapo mantha. Ngati ndinati, Mundipatse? Kapena, Muperekeko kwa ine chuma chanu? Kapena, Mundilanditse m'dzanja la mdani? Kapena, Mundiombole m'dzanja la oopsa? Mundilangize, ndipo ndidzakhala chete ine; mundizindikiritse umo ndinalakwira. Mau oongoka si ndiwo amphamvu? Koma kudzudzula kwanu mudzudzula chiyani? Kodi muyesa kudzudzula mau? Popeza maneno a munthu wodololoka akunga mphepo. Indetu, mugwetsera wamasiye msampha, mumkumbira bwenzi lanu mbuna. Koma tsopano balindani, mundipenyerere; ndikanena bodza pamaso panu mudzalizindikira. Bwererani, ndikupemphani, musandiipsire mlandu; inde, bwereraninso mlandu wanga ngwolungama. Kodi pali chosalungama palilime panga? Ngati sindizindikira zopanda pake m'kamwa mwanga? Kodi munthu alibe nkhondo kunja kuno? Kodi masiku ake sakunga masiku a wolembedwa ntchito? Monga kapolo woliralira mthunzi, monga wolembedwa ntchito ayembekezera mphotho yake, momwemo anandilowetsa miyezi yopanda pake. Nandiikiratu zowawa usiku ndi usiku. Ndigona pansi, ndikuti, Ndidzauka liti? Koma usiku undikulira; ndipo ndimapalapata mpaka mbandakucha. Mnofu wanga wavala mphutsi ndi nkanambo zadothi; khungu langa lang'ambika, nilinyansa. Masiku anga afulumira koposa mphindo ya muomba, apitirira opanda chiyembekezo. Kumbukira kuti moyo wanga ndiwo mphepo, diso langa silidzaonanso chokoma. Diso la amene andiona silidzandionanso, maso ako adzandipenyetsetsa, koma ine palibe. Mtambo wapita watha, momwemo wakutsikira kumanda sadzakwerakonso. Sadzabweranso kunyumba yake, osamdziwanso malo ake. Potero sindidzaletsa pakamwa panga; ndidzalankhula popsinjika mu mzimu mwanga; ndidzadandaula pakuwawa mtima wanga. Ndine nyanja kodi, kapena chinjoka cha m'nyanja, kuti Inu mundiikira odikira? Ndikati, Pakama panga mpondisangalatsa, pogona panga padzachepsa chondidandaulitsa; pamenepo mundiopsa ndi maloto, nimundichititsa mantha ndi masomphenya; potero moyo wanga usankha kupotedwa, ndi imfa, koposa mafupa anga awa. Ndinyansidwa nao moyo wanga; sindidzakhala ndi moyo chikhalire; mundileke; pakuti masiku anga ndi achabe. Munthu ndani kuti mumkuze, ndi kuti muike mtima wanu pa iye, ndi kuti mucheze naye m'mawa ndi m'mawa, ndi kumuyesa nthawi zonse? Mukana kundichokera kufikira liti, kapena kundileka mpaka nditameza dovu? Ngati ndachimwa, ndingachitire Inu chiyani, Inu wodikira anthu? Mwandiikiranji ndikhale chandamali chanu? Kuti ndikhale kwa ine ndekha katundu? Mulekeranji kukhululukira kulakwa kwanga ndi kundichotsera mphulupulu yanga? Popeza tsopano ndidzagona kufumbi; mudzandifunafuna, koma ine palibe. Pamenepo anayankha Bilidadi Msuki, nati, Udzanena izi kufikira liti? Ndipo mau a pakamwa pako adzakhala ngati namondwe kufikira liti? Ngati Mulungu akhotetsa chiweruzo? Ngati Wamphamvuyonse akhotetsa mlandu? Chinkana ana ako anamchimwira Iye, ndipo anawapereka mwa kulakwa kwao; koma ukafunitsitsa Mulungu, ndi kupembedza Wamphamvuyonse; ukakhala woyera ndi woongoka mtima, zoonadi adzakugalamukira tsopano, ndi kupindulitsa pokhala pako polungama. Ndipo chinkana chiyambi chako chinali chaching'ono, chitsiriziro chako chidzachuluka kwambiri. Pakuti ufunsire tsono mbadwo wapitawo, nusamalire zimene makolo ao adazisanthula. Pakuti ife ndife adzulo, osadziwa kanthu, popeza masiku athu a pa dziko lapansi ndiwo ngati mthunzi; amene aja sangakuphunzitse, ndi kukufotokozera, ndi kutulutsa mau a mumtima mwao? Ngati gumbwa aphuka popanda chinyontho? Ngati manchedza amera popanda madzi? Akali auwisi, sanawacheke, auma, asanaume mathengo onse ena. Momwemo mayendedwe a onse oiwala Mulungu; ndi chiyembekezo cha onyoza Mulungu; chidzatayika. Kulimbika mtima kwake kudzathyoka, chikhulupiriro chake chikunga nyumba ya kangaude. Adzatsamira nyumba yake, koma yosamlimbira; adzaiumirira koma yosakhalitsa. Akhala wamuwisi pali dzuwa, ndi nthambi zake zitulukira pamunda pake. Mizu yake iyangayanga pa kasupe wamadzi, apenyerera pokhalapo miyala. Akamuononga kumchotsa pamalo pake, padzamkana, ndi kuti, Sindinakuona. Taona, ichi ndicho chomkondweretsa panjira pake, ndi panthaka padzamera ena. Taona, Mulungu sakana munthu wangwiro; kapena kugwiriziza ochita zoipa. Koma adzadzaza m'kamwa mwako ndi kuseka, ndi milomo yako kufuula. Iwo akudana nawe adzavala manyazi; ndi hema wa oipa adzakhala kuli zii. Pamenepo Yobu anayankha, nati, Zoona, ndidziwa kuti chili chotero. Koma munthu adzakhala wolungama bwanji kwa Mulungu? Akafuna Iye kutsutsana naye, sadzambwezera Iye mau amodzi onse mwa chikwi. Ndiye wa mtima wanzeru, ndi wa mphamvu yaikulu; ndaniyo anadziumitsa mtima pa Iye, nakhala nao mtendere? Ndiye amene asuntha mapiri, osachidziwa iwo, amene amagubuduza mu mkwiyo wake. Amene agwedeza dziko lapansi lichoke m'malo mwake, ndi mizati yake injenjemere. Amene alamulira dzuwa ndipo silituluka, nakomera nyenyezi chizindikiro chakuzitsekera. Woyala thambo yekha, naponda pa mafunde a panyanja. Wolenga Mlalang'amba, Akamwiniatsatana, ndi Nsangwe, ndi Kumpotosimpita. Wochita zazikulu zosasanthulika, ndi zodabwitsa zosawerengeka. Taona, Mulungu apita pali ine, koma sindimpenya; napitirira, koma osamzindikira ine. Taona, akwatula, adzambwezetsa ndani? Adzanena naye ndani, Mulikuchita chiyani? Mulungu sadzabweza mkwiyo wake; athandizi odzikuza awerama pansi pa Iye. Nanga ine tsono ndidzamyankha bwanji, ndi kusankha mau anga akutsutsana ndi Iye? Ameneyo, chinkana ndikadakhala wolungama, sindikadamyankha; ndikadangompembedza wondiweruza ine. Ndikadaitana, ndipo akadayankha Iye, koma sindikadakhulupirira kuti Iye wamvera mau anga. Pakuti andithyola ndi mkuntho, nachulukitsa mabala anga kopanda chifukwa. Sandilola kuti ndipume, koma andidzaza ndi zowawa. Tikanena za mphamvu, si ndiye wamphamvu? Tikanena za kuweruza, adzamuitana ndani? Chinkana ndikhala wolungama, pakamwa panga padzanditsutsa; chinkana ndikhala wangwiro, padzanditsutsa wamphulupulu. Chinkana ndikhala wangwiro, sindidzisamalira mwini, ndipeputsa moyo wanga. Kuli chimodzimodzi monsemo, m'mwemo ndikuti Iye aononga wangwiro ndi woipa pamodzi. Mkwapulo ukapha modzidzimutsa, adzaseka tsoka la wosachimwa. Dziko lapansi laperekedwa m'dzanja la woipa; aphimba maso a oweruza ake. Ngati sindiye, pali yaninso? Tsopano masiku anga afulumira kuposa wamtokoma; athawa osaona chokoma. Apitirira ngati zombo zaliwiro; ngati mphungu igudukira chakudya chake. Ndikati, Ndidzaiwala chondidandaulitsa, ndidzasintha nkhope yanga yachisoni, ndidzasekerera. Pamenepo ndiopa zisoni zanga zonse, ndidziwa kuti simudzandiyesa wosachimwa. Mlandu udzanditsutsa; potero ndigwire ntchito chabe chifukwa ninji? Ndikasamba madzi a chipale chofewa ndi kuyeretsa manja anga ndi sopo. Mudzandiviikanso muli zoola, ndi zovala zanga zidzanyansidwa nane. Pakuti sindiye munthu, monga ine, kuti ndimyankhe. Kuti tikomane mlandu. Palibe wakutiweruza, wakutisanjika ife tonse awiri manja ake. Andichotsere ndodo yake, choopsa chake chisandichititse mantha; kuti ndinene, osamuopa, pakuti sinditero monga umo ndili. Mtima wanga ulema nao moyo wanga, ndidzadzilolera kudandaula kwanga, ndidzalankhula pakuwawa mtima wanga. Ndidzati kwa Mulungu, Musanditsutse; mundidziwitse chifukwa cha kutsutsana nane. Chikukomerani kodi kungosautsa, kuti mupeputsa ntchito yolemetsa manja anu, ndi kuti muwalira pa uphungu wa oipa? Muli nao maso a thupi kodi? Mupenya kodi monga umo apenyera munthu? Masiku anu akunga masiku a munthu kodi, zaka zanu zikunga masiku a munthu; kuti mufunsa mphulupulu yanga, ndi kulondola choipa changa; chinkana mudziwa kuti sindili woipa, ndipo palibe wakupulumutsa m'dzanja lanu? Manja anu anandiumba, nandiulunga monsemu, koma mufuna kundiononga. Mukumbukire kuti mwandiumba ngati dothi; ndipo kodi mudzandibwezera kufumbi? Simunanditsanula kodi ngati mkaka, ndi kundilimbitsa ngati mase? Munandiveka khungu ndi mnofu, ndi kundilumikiza mafupa ndi mitsempha. Mwandipatsa moyo, ndi kundikomera mtima, ndi masamalidwe anu anasunga mzimu wanga. Koma izi munazibisa mumtima mwanu; ndidziwa kuti ichi muli nacho. Ndikachimwa mundipenya; ndipo simudzandimasula mphulupulu yanga. Ndikakhala woipa, tsoka ine; ndikakhala wolungama, sindidzakweza mutu wanga; ndadzazidwa ndi manyazi, koma penyani kuzunzika kwanga. Ndipo mutu wanga ukadzikweza, mundisaka ngati mkango; mubweranso ndi kudzionetsera modabwitsa kwa ine. Mundikonzeranso mboni zonditsutsa, ndi kundichulukitsira mkwiyo wanu; nkhondo yobwerezabwereza yandigwera. Potero munandibadwitsa chifukwa ninji? Mwenzi nditapereka moyo wanga, lisanandione diso. Ndikadakhala monga ngati sindikadakhala; akadanditenga pobadwapo kunka nane kumanda. Masiku anga satsala owerengeka nanga? Lindani. Bandilekani kuti nditsitsimuke pang'ono, ndisanachoke kunka kumene sindikabweranso, ku dziko la mdima ndi la mthunzi wa imfa. Dziko la mdima bii ngati mdima wandiweyani, dziko la mthunzi wa imfa losalongosoka, kumene kuunika kukunga mdima. Pamenepo anayankha Zofari wa ku Naama, nati, Kodi mau ochulukawa sayenera kuwayankha? Ndi munthu wa milomo ayenera kuyesedwa wolungama? Kodi zotamanda zako ziwatseke anthu pakamwa? Useka kodi, wopanda munthu wakukuchititsapo manyazi? Pakuti unena, Chiphunzitso changa nchoona, ndipo ndili woyera pamaso pako. Koma, ha? Mwenzi atanena Mulungu, ndi kukutsegulira milomo yake motsutsa; nakufotokozere zinsinsi za nzeru, popeza zipindikapindika machitidwe ao! Chifukwa chake dziwa kuti Mulungu akuiwalira mphulupulu zina. Kodi ukhoza kupeza Mulungu mwa mufunafuna? Ukhoza kupeza Wamphamvuyonse motsindika? Kumpeza kutalika ngati kumwamba, ungachitenji? Kuzama ngati kumanda, ungadziwenji? Muyeso wake utalikira utali wake wa dziko lapansi, chitando chake chiposa cha nyanja. Akapita, nakatsekera, nakatulutsa bwalo la mlandu, adzamletsa ndani? Pakuti adziwa anthu opanda pake, napenyanso mphulupulu, ngakhale saisamalira. Koma munthu wopanda pake asowa nzeru, ngakhale munthu abadwa ngati mwanawabulu. Ukakonzeratu mtima wako, ndi kumtambasulira Iye manja ako; Mukakhala mphulupulu m'dzanja lako, uichotseretu kutali, ndi chisalungamo chisakhale m'mahema mwako. Popeza pamenepo udzakweza nkhope yako opanda banga; nudzalimbika osachita mantha; pakuti udzaiwala chisoni chako, udzachikumbukira ngati madzi opita. Ndipo moyo wako udzayera koposa usana; kungakhale kuli mdima kudzakhala ngati m'mawa. Ndipo udzalimbika mtima popeza pali chiyembekezo; nudzafunafuna, ndi kugona mosatekeseka. Inde udzagona pansi, wopanda wina wakukunjenjemeretsa, ndipo ambiri adzakupembedza. Koma maso a oipa adzagoma, ndi pothawirapo padzawasowa, ndipo chiyembekezo chao ndicho kupereka mzimu wao. Pamenepo Yobu anayankha, nati, Zoonadi inu ndinu anthu, ndi nzeru idzafa pamodzi ndi inu. Koma inenso ndili nayo nzeru monga inu. Sindingakuchepereni; ndani sadziwa zonga izi? Ndine ngati munthu wosekedwa ndi mnansi wake, ndinaitana kwa Mulungu, ndipo anandiyankha; munthu wolungama wangwiro asekedwa. Munthu wosatekeseka apeputsa tsoka mumtima mwake, limlindira woterereka mapazi ake. Mahema a achifwamba akhala mumtendere, ndi iwo oputa Mulungu alimbika mtima; amene Mulungu amadzazira dzanja lao. Tafunsira tsono kwa nyamazo, zidzakulangiza, ndi mbalame za m'mlengalenga, zidzakuuza. Kapena ulankhule ndi dziko lapansi, lidzakulangiza; ndi nsomba za kunyanja, zidzakufotokozera. Ndaniyo sadziwa nazo izi zonse; kuti dzanja la Yehova lichita ichi? M'dzanja mwake muli mpweya wa zamoyo zonse, ndi mzimu wa munthu aliyense. M'khutumu simuyesa mau, monga m'kamwa mulawa chakudya chake? Kwa okalamba kuli nzeru, ndi kwa a masiku ochuluka luntha. Kwa Iye kuli nzeru ndi mphamvu; uphungu ndi luntha ali nazo. Taona, agamula, ndipo palibe kumanganso; amtsekera munthu, ndipo palibe kumtsegulira. Taona atsekera madzi, naphwa; awatsegulira, ndipo akokolola dziko lapansi. Kwa Iye kuli mphamvu ndi nzeru. Wonyengedwa ndi wonyenga yemwe ali ake. Apita nao maphungu atawafunkhira, napulukiritsa oweruza milandu. Amasula chomangira cha mafumu, nawamangira nsinga m'chuuno mwao. Apita nao, ansembe atawafunkhira, nagubuduza amphamvu. Amchotsera wokhulupirika kunena kwake. Nalanda luntha la akulu. Atsanulira mnyozo pa akalonga, nawansezera olimba lamba lao. Avumbulutsa zozama mumdima, natulutsa mthunzi wa imfa ukhale poyera; achulukitsa amitundu, nawaononganso; abalalikitsa amitundu, nawabwezanso. Awachotsera akulu a anthu a padziko mtima wao, nawasokeretsa m'chipululu chopanda njira. Iwo ayambasa mumdima mopanda kuunika, ndipo awayendetsa dzandidzandi. Taonani, diso langa lachiona chonsechi; m'khutu mwanga ndachimva ndi kuchizindikira. Chimene muchidziwa inu, inenso ndichidziwa; sindikucheperani. Koma ine ndidzanena ndi Wamphamvuyonse, ndipo ndifuna kudzikanira kwa Mulungu. Koma inu ndinu opanga zabodza, asing'anga opanda pake inu nonse. Mwenzi mutakhala chete konse, ndiko kukadakhala nzeru zanu. Tamvani tsono kudzikanira kwanga, tamverani kudzinenera kwa milomo yanga. Kodi munenera Mulungu mosalungama, ndi kumnenera Iye monyenga? Kodi mukhalira kumodzi ndi Iye? Mundilimbirana mwa Mulungu. Nchokoma kodi kuti Iye akusanthuleni? Kodi mudzamnyenga Iye monga munyenga munthu? Adzakudzudzulani ndithu, mukachita tsankho m'tseri. Ukulu wake sukuchititsani mantha, ndi kuopsa kwake sikukugwerani kodi? Zikumbutso zanu ndizo miyambi ya mapulusa; zodzikanira zanu zikunga malinga adothi. Khalani chete, ndilekeni, kuti ndinene, chondifikira chifike. Ndilumirenji mnofu wanga pamano panga, ndi kupereka moyo wanga m'dzanja langa? Angakhale andipha koma ndidzamlindira; komanso ndidzaumirira mayendedwe anga pamaso pake. Iye adzakhalanso chipulumutso changa, pakuti wonyoza Mulungu sadzafika pamaso pake. Mvetsetsani mau anga, ndi kunenetsa kwanga kumveke m'makutu mwanu. Taonani tsono, ndalongosola mlandu wanga; ndidziwa kuti adzandimasula ndili wolungama. Ndaniyo adzatsutsana nane? Ndikakhala chete, ndidzapereka mzimu wanga. Zinthu ziwiri zokha musandichitire, pamenepo sindidzabisalira nkhope yanu. Mundichotsere dzanja lanu kutali, ndi kuopsa kwanu kusandichititse mantha. Pamenepo muitane, ndipo ndidzayankha; kapena ndinene ndine, ndipo mundiyankhe ndinu. Mphulupulu zanga ndi zochimwa zanga ndi zingati? Mundidziwitse kulakwa kwanga ndi tchimo langa. Mubisiranji nkhope yanu, ndi kundiyesa mdani wanu? Kodi mudzaopsa tsamba lakungouluka, ndi kulondola ziputu zouma? Pakuti mundilembera zinthu zowawa, ndi kundipatsa ngati cholowa mphulupulu za ubwana wanga. Mulonganso mapazi anga m'zigologolo, ndi kupenyerera mayendedwe anga onse; mudzilembera malire mopanika mapazi anga. Momwemo munthu akutha ngati chinthu choola, ngati chovala chodyedwa ndi njenjete. Munthu wobadwa ndi mkazi ngwa masiku owerengeka, nakhuta mavuto. Atuluka ngati duwa, nafota; athawa ngati mthunzi, osakhalitsa. Ndipo kodi mumtsegulira maso anu wotereyo, ndi kunditenga kunena nane mlandu Inu? Adzatulutsa choyera m'chinthu chodetsa ndani? Nnena mmodzi yense. Popeza masiku ake alembedwa, chiwerengo cha miyezi yake chikhala ndi Inu, ndipo mwamlembera malire ake kuti asapitirirepo iye; mumleke osamthira maso, kuti apumule, kuti akondwere nalo tsiku lake monga wolembedwa ntchito. Pakuti akaulikha mtengo pali chiyembekezo kuti udzaphukanso, ndi kuti nthambi yake yanthete siidzasowa. Ngakhale muzu wake wakalamba m'nthaka, ndi tsinde lake likufa pansi. Koma pa mnunkho wa madzi udzaphuka, nudzaswa nthambi ngati womera. Koma munthu akufa atachita liondeonde inde, munthu apereka mzimu wake, ndipo ali kuti? Madzi achoka m'nyanja, ndi mtsinje ukuphwa, nuuma; momwemo munthu agona pansi, osaukanso; kufikira miyamba kulibe, sadzaukanso, kapena kuutsidwa pa tulo take. Ha? Mukadandibisa kumanda, mukadandisunga m'tseri, mpaka wapita mkwiyo wanu. Mukadandiikira nthawi, ndi kundikumbukira. Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi? Ndikadayembekeza masiku onse a nkhondo yanga, mpaka kwafika kusandulika kwanga. Mukadaitana, ndipo ndikadakuyankhani; mukadakhumba ntchito ya manja anu. Koma tsopano muwerenga moponda mwanga; kodi simuyang'anitsa tchimo langa? Cholakwa changa chaikidwa m'thumba lokhomedwa chizindikiro; ndipo mumanga pamodzi mphulupulu zanga. Ndipo zoonadi, likagwa phiri, latha; ndi thanthwe lisunthika m'malo mwake. Madzi anyenya miyala; zosefukira zao zikokolola fumbi la nthaka; ndipo muononga chiyembekezo cha munthu. Mumlaka chilakire, napita iye; musintha nkhope yake, mumuuza achoke. Ana ake aona ulemu osadziwa iye; napeputsidwa, koma osazindikira za iwo. Koma thupi lake limuwawira yekha, ndi mtima wake umliritsa yekha. Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha, nati, Kodi mwini nzeru ayankhe ndi kudziwa kouluzika, ndi kudzaza mimba yake ndi mphepo ya kum'mawa? Kodi atsutsane ndi mnzake ndi mau akusathandiza? Kapena ndi maneno akusaphindulitsa? Zedi uyesa chabe mantha, nuchepsa chilingiriro pamaso pa Mulungu. Pakuti pakamwa pako paphunzitsa mphulupulu zako, nusankha lilime la ochenjerera. Pakamwa pako pakutsutsa, si ine ai. Inde milomo yako ikuchitira umboni wakukutsutsa. Kodi ndiwe munthu woyamba kubadwa? Kapena unayamba kulengedwa ndiwe, osati mapiri? Kodi unamva uphungu wachinsinsi wa Mulungu? Ndipo unadzikokera nzeru kodi? Udziwa chiyani, osachidziwa ife? Uzindikira chiyani, chosakhala mwa ife? Pakati pa ife pali aimvi, ndi okalambitsa, akuposa atate wako masiku ao. Masangalatso a Mulungu akuchepera kodi? Kapena uli nacho chinsinsi kodi? Mtima wako usonthokeranji nawe? Maso ako aphethiraphethira chifukwa ninji? Kuti utembenuza mzimu wako utsutsane ndi Mulungu, ndi kulola mau otere atuluke m'kamwa mwako. Munthu nchiyani kuti akhale woyera, wobadwa ndi mkazi kuti akhale wolungama? Taona, Mulungu sakhulupirira opatulika ake; ngakhale m'mwamba simuyera pamaso pake. Koposa kotani nanga munthu wonyansa ndi wodetsa, wakumwa chosalungama ngati madzi. Ndidzakuonetsa, undimvere; chimene ndinachiona, ndidzakufotokozera; chimene adachinena anzeru, adachilandira kwa makolo ao, osachibisa; ndiwo amene analandira okha dzikoli, wosapita mlendo pakati pao. Munthu woipa adzipweteka masiku ake onse, ndi zaka zowerengeka zisingikira woopsa. M'makutu mwake mumveka zoopsetsa; pali mtendere amfikira wakumuononga. Sakhulupirira kuti adzatulukamo mumdima, koma kuti lupanga limlindira. Ayendayenda ndi kufuna chakudya, nati, Chilikuti? Adziwa kuti lamkonzekeratu pafupi tsiku lamdima. Nsautso ndi chipsinjo zimchititsa mantha, zimlaka ngati mfumu yokonzekeratu kunkhondo. Pakuti amtambasula dzanja lake moyambana ndi Mulungu, napikisana ndi Wamphamvuyonse. Amthamangira Iye mwaliuma, ndi zikopa zake zochindikira. Popeza anakuta nkhope yake ndi kunenepa kwake, nachita mafunyenye a mafuta m'zuuno zake; adzakhala m'midzi yopasuka, m'nyumba zosakhalamo munthu, zoti zisandulika muunda. Sadzakhala wolemera, ndi chuma chake sichidzakhalitsa, ndi zipatso zake sizidzachuluka padziko. Sadzachoka mumdima; lawi la moto lidzaumitsa nthambi zake; ndipo adzachoka ndi mpumo wa m'kamwa mwake. Asatame zopanda pake, kudzinyenga nazo; pakuti zopanda pake zidzakhala chombwezera chake. Chidzachitika isanadze nthawi yake; pakuti nthambi yake siidzaphuka. Adzayoyoka zipatso zake zosapsa ngati mpesa, nadzathothoka maluwa ake ngati mtengo wa azitona. Pakuti msonkhano wa onyoza Mulungu udzakhala chumba, ndi moto udzapsereza mahema a olandira chokometsera mlandu. Aima ndi chovuta, nabala mphulupulu, ndi m'mimba mwao mukonzeratu chinyengo. Pamenepo Yobu anayankha, nati, Ndamva zambiri zotere; inu nonse ndinu otonthoza mtima mondilemetsa. Kodi adzatha mau ouluzika? Kapena chikuwindula nchiyani kuti uyankha zotere? Inenso ndikadanena monga inu, moyo wanu ukadakhala m'malo mwa moyo wanga, ndikadalumikizanitsa mau akutsutsana nanu, ndi kukupukusirani mutu wanga. Koma ndikadakulimbikitsani ndi m'kamwa mwanga, ndi chitonthozo cha milomo yanga chikadatsitsa chisoni chanu. Chinkana ndinena chisoni changa sichitsika; ndipo ndikaleka, chindichokera nchiyani? Koma tsopano wandilemetsa Iye; mwapasula msonkhano wanga wonse. Kundigwira kwanu, ndiko umboni wonditsutsa, kuonda kwanga kundiukira, kuchita umboni pamaso panga. Iye ananding'amba m'kundida kwake, nakwiya nane, anandikukutira mano; mdani wanga ananditong'olera maso ake. Iwo anandiyasamira pakamwa pao; anandiomba pama ndi kunditonza; asonkhana pamodzi kunditsutsa. Mulungu andipereka kwa osulangama, nandiponya m'manja a oipa. Ndinali mkupuma, koma anandithyola; inde anandigwira pakhosi, nandiphwanya; nandiimika ndikhale chandamali. Eni mauta ake andizinga, ang'amba impso zanga, osazileka; natsanulira pansi ndulu yanga. Andipasulapasula; andithamangira ngati wamphamvu. Ndadzisokerera chiguduli kukhungu langa. Ndipo ndaipsa mphamvu yanga m'fumbi. Nkhope yanga njodetsedwa ndi kulira misozi, ndi pa zikope zanga pali mthunzi wa imfa; pangakhale palibe chiwawa m'manja mwanga, ndi pemphero langa ndi loyera. Dziko iwe, usakwirire mwazi wanga, ndi kulira kwanga kusowe popumira. Tsopanonso, taona, mboni yanga ili kumwamba, ndi nkhoswe yanga ikhala m'mwamba. Mabwenzi anga andinyoza; koma diso langa lilirira misozi kwa Mulungu. Ha? Munthu akadapembedzera mnzake kwa Mulungu, monga munthu apembedzera mnansi wake! Pakuti zitafika zaka zowerengeka, ndidzamuka kunjira imene sindibwererako. Mzimu wanga watha, masiku anga afafanizika, kumanda kwandikonzekeratu. Zoonadi, ali nane ondiseka; ndi diso langa lili chipenyere m'kundiwindula kwao. Mupatse chigwiriro tsono, mundikhalire chikole Inu nokha kwanu; ndani adzapangana nane kundilipirira? Pakuti mwabisira mtima wao nzeru; chifukwa chake simudzawakuza. Iye wakupereka mabwenzi ake ku ukapolo, m'maso mwa ana ake mudzada. Anandiyesanso nthanthi za anthu; ndipo ndakhala ngati munthu womthira malovu pankhope pake. M'diso mwanga muchita chizirezire chifukwa cha chisoni, ndi ziwalo zanga zonse zilibe chithunzi. Anthu oongoka mtima adzadabwa nacho, ndi munthu wosalakwa adzadziutsa kumtsutsa wonyoza Mulunguyo. Koma wolungama asungitsa njira yake, ndi iye wa manja oyera adzakulabe mumphamvu. Koma bwerani inu nonse, idzani tsono; pakuti sindipeza mwa inu wanzeru. Masiku anga apitirira, zolingirira zanga zaduka, zakezake zomwe za mtima wanga. Zisanduliza usiku ukhale usana; kuunika kuyandikana ndi mdima. Ndikayembekezera kumanda kukhale nyumba yanga; ndikayala pogona panga mumdima. Ndikati kwa dzenje, Ndiwe atate wanga; kwa mphutsi, Ndiwe mai wanga ndi mlongo wanga; chilikuti chiyembekezo changa? Inde, chiyembekezo changa adzachiona ndani? Chidzatsikira kumipingiridzo ya kumanda, pamene tipumulira pamodzi kufumbi. Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha, nati, Musaka mau kufikira liti? Zindikirani, ndi pamenepo tidzanena. Tiyesedwa bwanji ngati nyama za kuthengo, ndi kukhala odetsedwa pamaso panu? Iwe wodzing'amba mumkwiyo mwako, kodi dziko lapansi lisiyidwe chifukwa cha iwe? Kapena thanthwe lisunthike m'malo mwake? Inde, kuunika kwa woipa kudzazima, ndi lawi la moto wake silidzawala. Kuunikaku kudzada m'hema mwake, ndi nyali yake ya pamwamba pake idzazima. Mapondedwe ake amphamvu adzasautsidwa, ndi uphungu wakewake udzamgwetsa. Pakuti aponyedwa m'ukonde ndi mapazi ake, namaponda pamatanda. Msampha udzamgwira kuchitende, ndi khwekhwe lidzamkola. Msampha woponda umbisikira pansi, ndi msampha wa chipeto panjira. Zoopetsa zidzamchititsa mantha monsemo, nadzampirikitsa kumbuyo kwake. Njala idzatha mphamvu yake, ndi tsoka lidzamkonzekeratu pambali pake. Zidzatha ziwalo za thupi lake, mwana woyamba wa imfa adzatha ziwalo zake. Adzazulidwa kuhema kwake kumene anakhulupirira; nadzatengedwa kunka naye kwa mfumu ya zoopsa. Adzakhala m'hema mwake iwo amene sali ake; miyala ya sulufure idzawazika pokhala pake. Mizu yake idzauma pansi, ndi nthambi yake idzafota m'mwamba. Chikumbukiro chake chidzatayika m'dziko, ndipo adzasowa dzina kukhwalala. Adzamkankha achoke kukuunika alowe kumdima; adzampirikitsa achoke m'dziko lokhalamo anthu. Sadzakhala naye mwana kapena chidzukulu mwa anthu a mtundu wake, kapena wina wotsalira kumene anakhalako. Akudza m'mbuyo adzadabwa nalo tsiku lake, monga aja omtsogolera anagwidwa mantha. Zoonadi, zokhalamo osalungama zitero, ndi malo a iye amene sadziwa Mulungu ndi awa. Koma Yobu anayankha, nati, Mudzasautsa moyo wanga kufikira liti, ndi kundithyolathyola nao mau? Kakhumi aka mwandichititsa manyazi; mulibe manyazi kuti mundiumira mtima. Ndipo ngati ndalakwa ndithu, kulakwa kwanga kuli ndi ine ndekha. Ngati inu mudzikuza ndithu pa ine, ndi kunditchulira mtonzo wanga kuti munditsutse nao. Dziwani tsopano kuti Mulungu wandikhotetsera mlandu wanga, nandizinga ndi ukonde wake. Taonani, ndifuula kuti, Chiwawa! Koma sandimvera; ndikuwa, koma palibe chiweruzo. Iye ananditsekera njira kuti ndisapitireko, naika mdima poyendapo ine. Anandivula ulemerero wanga, nandichotsera korona pamutu panga. Nandigamula ponsepo, ndipo ndamukatu; nachizula chiyembekezo changa ngati mtengo. Wandiyatsiranso mkwiyo wake, nandiyesera ngati wina wa adani ake. Ankhondo ake andidzera pamodzi, nandiundira njira yao, nandimangira misasa pozinga hema wanga. Iye anandichotsera abale anga kutali, ndi odziwana nane andiyesa mlendo konse. Anansi anga andisowa, ndi odziwana nane bwino andiiwala. Iwo a m'nyumba mwanga ndi adzakazi anga andiyesa mlendo; ndine wachilendo pamaso pao. Ndikaitana kapolo wanga, sandibwezera mau, chinkana ndimpembedza pakamwa panga. Mpweya wanga unyansira mkazi wanga, chinkana ndinampembedza ndi kutchula ana a thupi langa. Angakhale ana ang'ono andipeputsa, ndikanyamuka, andinena; mabwenzi anga enieni onse anyansidwa nane; ndi onse ndakondana nao asandulika adani anga. Fupa langa laumirira pa khungu langa ndi mnofu wanga, ndipo ndapulumuka ndili nazo nkhama za mano anga. Ndichitireni chifundo, ndichitireni chifundo, mabwenzi anga inu; pakuti dzanja la Mulungu landikhudza. Mundilondola bwanji ngati Mulungu, losakukwanirani thupi langa? Ha! Akadalembedwa mau anga! Ha! Akadalembedwa m'buku! Akadawazokota pathanthwe chikhalire, ndi chozokotera chachitsulo ndi kuthira ntovu! Koma ndidziwa kuti Mombolo wanga ali ndi moyo, nadzauka potsiriza pafumbi. Ndipo khungu langa litaonongeka, pamenepo wopanda thupi langa, ndidzapenya Mulungu, amene ndidzampenya ndekha, ndi maso anga adzamuona, si wina ai. Imso zanga zatha m'kati mwanga. Mukati, Tiyeni timlondole! Popeza chifukwa cha mlandu chapezeka mwa ine; muchite nalo mantha lupanga; pakuti mkwiyo utenga zolakwa za lupanga, kuti mudziwe pali chiweruzo. Pamenepo anayankha Zofari Mnaama, nati, M'mwemo zolingirira zanga zindiyankha, chifukwa chake ndifulumidwa m'kati mwanga. Ndamva kudzudzula kwakundichititsa manyazi, ndi mzimu wa nzeru yanga undiyankha. Kodi suchidziwa ichi chiyambire kale lomwe, nuyambira anaika munthu pa dziko lapansi, kuti kufuula kokondwera kwa woipa sikukhalira kutha, ndi chimwemwe cha wonyoza Mulungu chikhala kamphindi? Chinkana ukulu wake ukwera kunka kuthambo, nugunda pamitambo mutu wake; koma adzatayika kosatha ngati zonyansa zake; iwo amene adamuona adzati, Ali kuti iye? Adzauluka ngati loto, osapezekanso; nadzaingidwa ngati masomphenya a usiku. Diso lidamuonalo silidzamuonanso; ndi malo ake sadzampenyanso. Ana ake adzapempha aumphawi awakomere mtima; ndi manja ake adzabweza chuma chake. Mafupa ake adzala nao unyamata wake, koma udzagona naye pansi m'fumbi. Chinkana choipa chizuna m'kamwa mwake, chinkana achibisa pansi pa lilime lake; chinkana achisunga, osachileka, nachikhalitsa m'kamwa mwake; koma chakudya chake chidzasandulika m'matumbo mwake, chidzakhala ndulu ya mphiri m'kati mwake. Anachimeza chuma koma adzachisanzanso; Mulungu adzachitulutsa m'mimba mwake. Adzayamwa ndulu ya mphiri; pakamwa pa njoka padzamupha. Sadzapenyerera timitsinje, toyenda nao uchi ndi mafuta. Chimene adagwiriracho ntchito, adzachibweza, osachimeza; sadzakondwera monga mwa zolemera zake adaziona. Pakuti anapsinja, nasiya aumphawi; analanda nyumba mwachiwawa, imene sanaimange. Popeza sanadziwe kupumula m'kati mwake, sadzalanditsa kanthu ka zofunika zake. Sikunatsalira kanthu kosadya iye, chifukwa chake zokoma zake sizidzakhalitsa. Pomkwanira kudzala kwake adzakhala m'kusauka; dzanja la yense wovutika lidzamgwera. Poti adzaze mimba yake, Mulungu adzamponyera mkwiyo wake waukali, nadzamvumbitsira uwu pakudya iye. Adzathawa chida chachitsulo, ndi muvi wa uta wamkuwa udzampyoza. Auzula, nutuluka m'thupi mwake; inde nsonga yonyezimira ituluka m'ndulu mwake; zamgwera zoopsa. Zamdima zonse zimsungikira zikhale chuma chake, moto wosaukoleza munthu udzampsereza; udzatha wotsalira m'hema mwake. M'mwamba mudzavumbulutsa mphulupulu yake, ndi dziko lapansi lidzamuukira. Phindu la m'nyumba mwake lidzachoka, akatundu ake adzamthawa tsiku la mkwiyo wake. Ili ndi gawo la munthu woipa, lochokera kwa Mulungu, ndi cholowa amuikiratu Mulungu. Pamenepo Yobu anayankha, nati, Mvetsetsani mau anga; ndi ichi chikhale chitonthozo chanu. Mundilole, ndinene nanenso; ndipo nditanena ine, sekani. Kodi ine, kudandaula kwanga, ndidandaulira munthu? Ndipo ndilekerenji kupsa mtima? Ndiyang'anireni, nimusumwe, gwirani pakamwa panu. Ndikangokumbukira ndivutika mtima, ndi thupi langa lichita nyaunyau. Oipa akhaliranji ndi moyo, nakalamba, nalemera kwakukulu? Mbeu zao zikhazikika pamodzi nao pankhope pao, ndi ana ao pamaso pao. Nyumba zao sizitekeseka ndi mantha, ngakhale ndodo ya Mulungu siiwakhalira. Ng'ombe yao yamphongo imakwera, yosakanika; ng'ombe yao yaikazi imaswa, yosapoloza. Atulutsa makanda ao ngati gulu, ndi ana ao amavinavina. Aimbira lingaka ndi zeze, nakondwera pomveka chitoliro. Atsekereza masiku ao ndi zokoma, natsikira m'kamphindi kumanda. Koma adati kwa Mulungu, Tichokereni; pakuti sitifuna kudziwa njira zanu. Wamphamvuyonse ndiye yani kuti timtumikire? Ndipo tidzapindulanji pakumpemphera Iye? Taonani, zokoma zao sizili m'dzanja lao; (koma uphungu wa oipa unditalikira.) Ngati nyali za oipa zizimidwa kawirikawiri? Ngati tsoka lao liwagwera? Ngati Mulungu awagawira zowawa mu mkwiyo wake? Ngati akunga ziputu zomka ndi mphepo, ngati mungu wouluzika ndi nkuntho? Mukuti, Mulungu asungira ana ake a munthu choipa chake, ambwezere munthuyo kuti achidziwe. Aone yekha chionongeko chake m'maso mwake, namwe mkwiyo wa Wamphamvuyonse. Pakuti chomsamalitsa nyumba yake nchiyani, atapita iye, chiwerengo cha miyezi yake chitadulidwa pakati? Ngati pali munthu wakumphunzitsa Mulungu nzeru? Popeza Iye aweruza mlandu iwo okwezeka. Wina akufa, wabiriwiri, ali chikhalire ndi chipumulire. Mbale zake zidzala ndi mkaka; ndi wongo wa m'mafupa ake uli momwe. Koma mnzake akufa ali nao mtima wakuwawa, osalawa chokoma konse. Iwo agona chimodzimodzi kufumbi, ndi mphutsi ziwakuta. Taonani, ndidziwa maganizo anu, ndi chiwembu mundilingirira moipa. Pakuti munena, Ili kuti nyumba ya kalonga? Ndi hema wokhalamo woipa ali kuti? Simunawafunsa kodi opita m'njira? Ndipo simusamalira zotsimikiza zao? Zakuti munthu woipa asungika tsiku la tsoka? Natulutsidwa tsiku la mkwiyo? Adzamfotokozera ndani njira yake pamaso pake? Nadzamlipitsa ndani pa ichi anachichita? Potsiriza pake adzapita naye kumanda, nadzadikira pamanda pake. Zibuma za kuchigwa zidzamkomera. Adzakoka anthu onse amtsate, monga anamtsogolera osawerengeka. Potero munditonthozeranji nazo zopanda pake, popeza m'mayankho mwanu mutsala mabodza okha? Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha, nati, Kodi munthu apindulira Mulungu? Koma wanzeru angodzipindulira yekha. Kodi Wamphamvuyonse akondwera nako kuti iwe ndiwe wolungama? Kapena kodi apindula nako kuti ukwaniritsa njira zako? Kodi akudzudzula, nadza nawe kumlandu, chifukwa cha kumuopa kwako? Zoipa zako sizichuluka kodi? Ndi mphulupulu zako sizikhala zosawerengeka kodi? Pakuti wamtenga chikole kwa mbale wako wopanda chifukwa, ndi kuvula ausiwa zovala zao. Sunampatsa wolema madzi amwe, ndi wanjala unammana chakudya. Koma munthu mwini mphamvu, dziko ndi lake; ndi munthu wovomerezeka, anakhala momwemo. Unabweza akazi amasiye osawaninkha kanthu, ndi manja a ana amasiye anathyoledwa. Chifukwa chake misampha ikuzinga. Ndi mantha akuvuta modzidzimutsa, kapena mdima kuti ungaone, ndi madzi aunyinji akumiza. Kodi Mulungu sakhala m'mwamba m'tali? Ndipo penyani kutalika kwake kwa nyenyezi, zili m'talitali. Ndipo ukuti, Adziwa chiyani Mulungu? Aweruza kodi mwa mdima wa bii? Mitambo ndiyo chomphimba, kuti angaone; ndipo amayenda pa thambo lakumwamba. Udzasunga kodi njira yakale, anaiponda anthu amphulupulu? Amene anakwatulidwa isanafike nyengo yao, chigumula chinakokolola kuzika kwao; amene anati kwa Mulungu, Tichokereni; ndipo, Angatichitire chiyani Wamphamvuyonse? Angakhale Iye adadzaza nyumba zao ndi zabwino; koma uphungu wa oipa unditalikira. Olungama achiona nakondwera; ndi osalakwa awaseka pwepwete, ndi kuti, Zoonadi, otiukirawo alikhidwa, ndi zowatsalira, moto unazipsereza. Uzolowerane ndi Iye, nukhale ndi mtendere; ukatero zokoma zidzakudzera. Landira tsono chilamulo pakamwa pake, nuwasunge maneno ake mumtima mwako. Ukabweranso kwa Wamphamvuyonse, udzamanga bwino; ukachotsera chosalungama kutali kwa mahema ako. Ndipo utaye chuma chako kufumbi, ndi golide wa ku Ofiri ku miyala ya kumitsinje. Ndipo Wamphamvuyonse adzakhala chuma chako, ndi ndalama zako zofunika. Pakuti pamenepo udzakondwera naye Wamphamvuyonse, ndi kuweramutsa nkhope yako kwa Mulungu. Udzampemphera ndipo adzakumvera; nudzatsiriza zowinda zako. Ukatsimikiza mtima kakuti, kadzakhazikikira iwe; ndi kuunika kudzawala pa njira zako. Anthu akakugwetsa pansi, udzati, Adzandikweza; ndipo adzapulumutsa wodzichepetsayo. Adzamasula ngakhale wopalamula, inde adzamasuka mwa kuyera kwa manja ako. Koma Yobu anayankha, nati, Lero lomwe kudandaula kwanga kumawawa; kulanga kwanga kuposa kubuula kwanga m'kulemera kwake. Ha! Ndikadadziwa kumene ndikampeza Mulungu, kuti ndifike kumpando wake! Ndikadalongosola mlandu wanga pamaso pake, ndikadadzaza m'kamwa mwanga ndi matsutsano. Ndikadadziwa mau akadandiyankha ine, ndikadazindikira chimene akadanena nane. Akadatsutsana nane kodi mwa mphamvu yake yaikulu? Iai, koma akadanditcherera khutu. Apo woongoka mtima akadatsutsana naye; ndipo ndikadapulumuka chipulumukire kwa Woweruza wanga. Taonani, ndikamka m'tsogolo, kulibe Iye; kapena m'mbuyo sindimzindikira; akachita Iye kulamanzere, sindimpenyerera; akabisala kulamanja, sindimuona. Koma adziwa njira ndilowayi; atandiyesa ndidzatuluka ngati golide. Phazi langa lagwiratu moponda Iye, ndasunga njira yake, wosapatukamo. Sindinabwerera kusiya malamulo a pa milomo yake; ndasungitsa mau a pakamwa pake koposa lamulo langalanga. Koma Iye ndiye wa mtima umodzi, adzambweza ndani? Ndi ichi chimene moyo wake uchifuna achichita. Pakuti adzachita chondiikidwiratu; ndipo zambiri zotere zili ndi Iye. Chifukwa chake ndiopsedwa pankhope pake; ndikalingirira, ndichita mantha ndi Iye. Pakuti Mulungu walefula mtima wanga, ndi Wamphamvuyonse wandiopsa. Popeza sindinalikhidwa usanafike mdimawo, ndipo sanandiphimbire nkhope yanga ndi mdima wa bii. Wamphamvuyonse alekeranji kuikiratu nyengo? Ndi iwo omdziwa alekeranji kudziwa masiku ake? Alipo akusendeza malire; alanda gulu la zoweta, nazidyetsa. Akankhizira kwao bulu wa amasiye, atenga ng'ombe ya mfedwa ikhale chikole. Apatukitsa aumphawi m'njira; osauka a padziko abisala pamodzi. Taonani, ngati mbidzi za m'chipululu atulukira kuntchito zao, nalawirira nkufuna chakudya; chipululu chiwaonetsera chakudya cha ana ao. Atema dzinthu zao m'munda; natola khunkha m'munda wampesa wa woipa. Agona amaliseche usiku wonse opanda chovala, alibe chofunda pachisanu. Avumbwa ndi mvula kumapiri, nafukata thanthwe posowa pousapo. Akwatula wamasiye kubere, natenga chikole chovala cha osauka; momwemo ayenda amaliseche opanda chovala, nasenza mtolo wa dzinthu ali ndi njala. M'kati mwa malinga a iwo aja ayenga mafuta; aponda mphesa moponderamo, namva ludzu. M'mudzi waukulu anthu abuula alinkufa; ndi moyo wa iwo olasidwa ufuula; koma Mulungu sasamalira choipacho. Iwo ndiwo amene apikisana nako kuunika, sadziwa njira zake, Sasunga mayendedwe ake. Kukacha auka wambanda, napha wosauka ndi waumphawi; ndi usiku asanduka mbala. Ndipo diso la wachigololo liyembekezera chisisira, ndi kuti, Palibe diso lidzandiona; navala chophimba pankhope pake. Kuli mdima aboola nyumba, usana adzitsekera, osadziwa kuunika. Pakuti iwo onse auyesa m'mawa mthunzi wa imfa; pakuti adziwa zoopsa za mthunzi wa imfa. Atengedwa ngati choyandama pamadzi; gawo lao litembereredwa padziko; sadzalunjikanso njira ya minda yamphesa. Chilala ndi dzuwa zitha madzi a chipale chofewa, momwemo manda achita nao ochimwa. M'mimba mudzamuiwala; mphutsi zidzamudya mokondwera. Sadzamkumbukiranso; ndipo chosalungama chidzathyoledwa ngati mtengo. Alusira chumba wosabala, osamchitira wamasiye chokoma. Mulungu awakhalitsa amphamvu mwa mphamvu yake; iwo aukanso m'mene anayesa kuti sadzakhala ndi moyo. Awalola akhale osatekeseka, ndipo alimbikapo; koma maso ake ali pa njira zao. Akwezeka; m'kamphindi kuli zii; inde atsitsidwa, achotsedwa monga onse ena, adulidwa ngati tirigu ngala zake. Ndipo ngati si kutero, anditsutsa ndani kuti ndili wabodza, ndi kuyesa mau anga opanda pake? Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha, nati, Kulamulira ndi kuopsa kuli ndi Iye; achita mtendere pa zam'mwamba zake. Ngati awerengedwa makamu ake? Ndipo ndaniyo, kuunika kwake sikumtulukira? Potero munthu akhala bwanji wolungama kwa Mulungu? Kapena wobadwa ndi mkazi akhala woyera bwanji? Taonani, ngakhale mwezi ulibe kuwala; ndi nyenyezi siziyera pamaso pake; kopambana kotani nanga munthu, ndiye mphutsi! Ndi wobadwa ndi munthu, ndiye nyongolotsi! Koma Yobu anayankha, nati, Wamthandiza bwanji wopanda mphamvu. Kulipulumutsa dzanja losalimba! Wampangira bwanji wopanda nzeruyu! Ndi kudziwitsa nzeru zenizeni mochuluka! Wafotokozera yani mau? Ndi mzimu wa yani unatuluka mwa iwe? Adafawo anjenjemera pansi pa madzi ndi zokhalamo. Kumanda kuli padagu pamaso pake, ndi kuchionongeko kusowa chophimbako. Ayala kumpoto popanda kanthu, nalenjeka dziko pachabe. Amanga madzi m'mitambo yake yochindikira; ndi mtambo sung'ambika pansi pake. Atchingira pa mpando wake wachifumu, nayalapo mtambo wake. Analembera madziwo malire, mpaka polekeza kuunika ndi mdima. Mizati ya thambo injenjemera, ndi kudabwa pa kudzudzula kwake. Mwa mphamvu yake agwetsa nyanja bata; ndipo mwa luntha lake akantha kudzikuza kwake. Mwa mzimu wake anyezimiritsa thambo; dzanja lake linapyoza njoka yothawayo. Taonani, awa ndi malekezero a njira zake; ndi chimene tikumva za Iye ndi chinong'onezo chaching'ono; koma kugunda kwa mphamvu yake akudzindikiritsa ndani? Ndipo Yobu anaonjezanso mwambi wake, nati, Pali Mulungu, amene anandichotsera zoyenera ine, ndi Wamphamvuyonse, amene anawawitsa moyo wanga, pakuti moyo wanga wonse ukali mwa ine, ndi mpweya wa Mulungu m'mphuno mwanga; milomo yanga siilankhula chosalungama, ndi lilime langa silitchula zachinyengo. Sindivomereza konse kuti muli olungama; mpaka kufa ine sinditaya ungwiro wanga. Ndiumirira chilungamo changa, osachileka; chikhalire moyo ine, mtima wanga sunditonza. Mdani wanga akhale ngati woipa, ndi iye amene andiukira ngati wosalungama. Pakuti chiyembekezo cha wonyoza Mulungu nchiyani pomlikhatu Mulungu, pomchotsera moyo wake? Kodi Mulungu adzamvera kufuula kwake, ikamdzera nsautso? Kodi adzadzikondweretsa naye Wamphamvuyonse, ndi kuitana kwa Mulungu nthawi zonse? Ndidzakulangizani za dzanja la Mulungu; chokhala ndi Wamphamvuyonse sindidzachibisa. Taonani, inu nonse munachiona; ndipo mugwidwa nazo zopanda pake chifukwa ninji? Ili ndi gawo la munthu woipa kwa Mulungu, ndi cholowa cha akupsinja anzao achilandira kwa Wamphamvuyonse. Akachuluka ana ake, ndiko kuchulukira lupanga, ndi ana ake sadzakhuta chakudya. Akumtsalira iye adzaikidwa muimfa, ndi akazi ake amasiye sadzalira maliro. Chinkana akundika ndalama ngati fumbi, ndi kukonzeratu zovala ngati dothi; azikonzeretu, koma wolungama adzazivala, ndi wosalakwa adzagawa ndalamazo. Amanga nyumba yake ngati kangaude, ndi ngati wolindira amanga dindiro. Agona pansi ali wachuma, koma saikidwa; potsegula maso ake, wafa chikomo. Zoopsa zimgwera ngati madzi; nkhuntho umtenga usiku. Mphepo ya kum'mawa imtenga, nachoka iye; nimkankha achoke m'malo mwake. Pakuti Mulungu adzamponyera zoopsa, osamleka; kuthawa akadathawa m'dzanja lake. Anthu adzamuombera manja, nadzamuimbira mluzu achoke m'malo mwake. Koma kuli mtapo wa siliva, ndi malo a golide amene amuyenga. Chitsulo achitenga m'nthaka, ndi mkuwa ausungunula kumwala. Munthu athawitsa mdima, nafunafuna mpaka malekezero onse, miyala ya mdima wa bii ndi ya mthunzi wa imfa. Aboola mgodi posiyana patali pokhala anthu; aiwalika ndi phazi lopitapo; apachikika kutali ndi anthu, nalendewalendewa. Kunena za nthaka, kuchokera momwemo mumatuluka chakudya, ndi m'munsi mwake musandulizika ngati ndi moto. Miyala yake ndiyo malo a safiro, ndipo ili nalo fumbi lagolide. Njira imeneyi palibe chiombankhanga chiidziwa; lingakhale diso la kabawi losapenyapo. Nyama zodzikuza sizinapondapo, ngakhale mkango waukali sunapitapo. Munthu atambasulira dzanja lake kumwala; agubuduza mapiri kuyambira kumizu. Asema njira pakati pa matanthwe, ndi diso lake liona chilichonse cha mtengo wake. Atseka mitsinje ingadonthe; natulutsira poyera chobisikachi. Koma nzeru, idzapezeka kuti? Ndi luntha, malo ake ali kuti? Munthu sadziwa mtengo wake; ndipo silipezeka m'dziko la amoyo. Pozama pakuti, Mwa ine mulibe; ndi nyanja ikuti, Kwa ine kulibe. Silipezeka ndi golide, sayesapo siliva mtengo wake. Sailinganiza ndi golide wa Ofiri, ndi sohamu wa mtengo wake wapatali kapena safiro. Golide ndi krustalo sizilingana nayo; ndi kusinthana kwake, siisinthanika ndi zisambiro za golide woyengetsa. Korali kapena ngale sizikumbukikapo. Mtengo wake wa nzeru uposa wa korali wofiira. Topazi wa Kusi sufanana nayo, sailinganiza ndi golide wolongosoka. Koma nzeru ifuma kuti? Ndi luntha, pokhala pake pali kuti? Popeza pabisikira maso a zamoyo zonse, pabisikiranso mbalame za m'mlengalenga. Chionongeko ndi Imfa zikuti, Tamva mbiri yake m'makutu mwathu. Mulungu ndiye azindikira njira yake, ndiye adziwa pokhala pake. Pakuti apenyerera malekezero a dziko lapansi, naona pansi pa thambo ponse; pamene anaikira mphepo muyeso wake, nayesera madzi miyeso; pakuchitira mvula lamulo, ndi njira yoyendamo mphezi ya bingu; pamenepo anaiona nzeru, naifotokozera; anaikonza, naisanthula. Koma kwa munthu anati, Taonani, kuopa Ambuye ndiko nzeru; ndi kupatukana nacho choipa ndiko luntha. Ndipo Yobu anaonjezanso mwambi wake, nati, Ha! Ndikadakhala monga m'miyezi yapitayi, monga m'masiku akundisunga Mulungu; muja nyali yake inawala pamutu panga, ndipo ndi kuunika kwake ndinayenda mumdima; monga umo ndinakhala m'masiku anga olimba, muja uphungu wa Mulungu unakhala pahema panga. Muja Wamphamvuyonse akali nane pamodzi, ndi ana anga anandizinga; muja popondera ine padakhatamira ndi mafuta amkaka, ndi thanthwe linanditsanulira mitsinje ya mafuta a azitona! Muja ndinatuluka kunka kuchipata kumudzi, muja ndinakonza pokhala panga kukhwalala, anyamata anandiona nabisala, okalamba anandinyamukira, nakhala chilili. Akalonga anadziletsa kulankhula, ndi kugwira pakamwa pao; mau a omveka anali zii, ndi lilime lao linamamatira kumalakalaka ao. Pakuti pondimva ine khutu, linandidalitsa; ndipo pondiona diso, linandichitira umboni. Pakuti ndinapulumutsa wozunzika wakufuula; mwana wamasiye yemwe wosowa mthandizi. Dalitso la iye akati atayike linandidzera, ndi mtima wa mkazi wamasiye ndinauimbitsa mokondwera. Ndinavala chilungamo, ndipo chinandivala ine; chiweruzo changa chinanga mwinjiro ndi nduwira. Ndinali maso a akhungu, ndi mapazi a otsimphina. Ndinali atate wa waumphawi; ndi mlandu wa iye amene sindinamdziwa ndinafunsitsa. Ndipo ndinathyola nsagwada ya wosalungama, ndi kukwatula chogwidwa kumano kwake. Pamenepo ndinati, Ndidzatsirizika m'chisa changa; ndipo ndidzachulukitsa masiku anga ngati mchenga. Muzu wanga watambalala kufikira kumadzi; ndi mame adzakhala pa nthambi yanga usiku wonse. Ulemu wanga udzakhala wosaguga mwa ine, ndi uta wanga udzakhala wosalifuka m'dzanja mwanga. Anthu anandimvera, nalindira, nakhala chete, kuti ndiwapangire. Nditanena mau anga sanalankhulenso, ndi kunena kwanga kunawakhera. Anandilindira ngati kulindira mvula, nayasama pakamwa pao ngati kulira mvula ya masika. Ndinawaseka akapanda kulimbika mtima; ndipo sanagwetse kusangalala kwa nkhope yanga. Ndinawasankhira njira yao ndi kukhala mkulu wao. Ndinakhala ngati mfumu mwa ankhondo ake, ngati wotonthoza ofedwa. Koma tsopano iwo osafikana msinkhu wanga andiseka, iwo amene atate ao ndikadawapeputsa, osawaika pamodzi ndi agalu olinda nkhosa zanga. Mphamvunso ya m'manja mwao ndikadapindulanji nayo? Ndiwo anthu amene unyamata wao udatha, atsala mafupa okhaokha ndi kusowa ndi njala; akungudza nthaka youma kuli mdima wa m'chipululu chopasuka. Atchera therere lokolera kuzitsamba, ndi chakudya chao ndicho mizu ya dinde. Anawapirikitsa pakati pa anthu, awafuulira ngati kutsata mbala. Azikhala m'zigwa za chizirezire, m'maenje a m'nthaka ndi m'mapanga. Pakati pa zitsamba alira ngati bulu, pansi pa khwisa asonkhana pamodzi. Ndiwo ana a opusa, inde ana a anthu opanda dzina; anawaingitsa kuwachotsa m'dziko. Koma tsopano ndasanduka nyimbo ya oterewo, nandiyesa nthanthi. Anyansidwa nane, akhala patali ndi ine, saleka kuthira malovu pankhope panga. Pakuti anamasula nsinga zao, nandizunza; anataya chomangira m'kamwa mwao pamaso panga. Kudzanja langa lamanja anauka oluluka, akankha mapazi anga, andiundira njira zao zakundiononga. Aipsa njira yanga, athandizana ndi tsoka langa; ndiwo anthu omwewo osowa mthandizi. Akudza ngati opitira pogamuka linga papakulu, pakati pa zopasuka adzigubuduza kundidzera ine. Anditembenuzira zondiopsa, auluza ulemu wanga ngati mphepo; ndi zosungika zanga zapita ngati mtambo. Ndipo tsopano moyo wanga udzitsanulira m'kati mwanga; masiku akuzunza andigwira. Nyengo ya usiku mafupa anga awaza mwa ine, ndi zowawa zondikungudza sizipuma. Mwa mphamvu yaikulu ya nthenda yanga chovala changa chinasandulika, chindithina ngati pakhosi pa malaya anga. Iye anandiponya m'matope, ndipo ndafanana ndi fumbi ndi phulusa. Ndifuula kwa Inu, koma simundiyankha; ndinyamuka, ndipo mungondipenyerera. Mwasandulika kundichitira nkharwe; ndi mphamvu ya dzanja lanu mundizunza. Mundikweza kumphepo, mundiyendetsa pomwepo; ndipo mundisungunula mumkuntho. Pakuti ndidziwa kuti mudzandifikitsa kuimfa, ndi kunyumba yokomanamo amoyo onse. Koma munthu akati agwe, satambasula dzanja lake kodi? Akati aonongeke, safuulako kodi? Kodi sindinamlirira misozi wakulawa zowawa? Kodi moyo wanga sunachitira chisoni osowa? Muja ndinayembekeza chokoma chinadza choipa, ndipo polindira kuunika unadza mdima. M'kati mwanga mupweteka mosapuma, masiku a mazunzo andidzera. Ndiyenda ndili wothimbirira osati ndi dzuwa ai; ndinyamuka mumsonkhano ndi kufuula. Ndili mbale wao wa ankhandwe, ndi mnansi wao wa nthiwatiwa. Khungu langa lada, nilindifundukira; ndi mafupa anga awawa ndi kutentha kwao. Chifukwa chake zeze wanga wasandulika wa maliro, ndi chitoliro changa cha mau a olira misozi. Ndinapangana ndi maso anga, potero ndipenyerenji namwali? Pakuti gawo la Mulungu lochokera kumwamba, ndi cholowa cha Wamphamvuyonse chochokera m'mwambamo nchiyani? Si ndizo chionongeko cha wosalungama, ndi tsoka la ochita mphulupulu? Nanga sapenya njira zanga, ndi kuwerenga moponda mwanga monse? Ngati ndinayanjana nalo bodza, ndi phazi langa linathamangira chinyengo; andiyese ndi muyeso wolingana, kuti Mulungu adziwe ungwiro wanga. Ngati phazi langa linapatuka m'njira, ndi mtima wanga unatsata maso anga? Ngati chilema chamamatira manja anga? Ndibzale ine nadye wina, ndi zondimerera ine zizulidwe. Ngati mtima wanga wakopeka ndi mkazi, ngati ndalalira pa khomo la mnzanga, mkazi wanga aperere wina; wina namuike kumbuyo. Pakuti icho ndi choipitsitsa, ndicho mphulupulu yoyenera oweruza anene mlandu wake. Pakuti ndicho moto wakunyeka mpaka chionongeko, ndi chakuzula zipatso zanga zonse. Ngati ndapeputsa mlandu wa kapolo wanga, kapena wa mdzakazi wanga, potsutsana nane iwo, ndidzatani ponyamuka Mulungu? Ndipo pondizonda Iye ndidzamnyankha chiyani? Kodi Iye amene anandilenga ine m'mimba sanamlenge iyenso? Sindiye mmodzi anatiumba m'mimba? Ngati ndakaniza aumphawi chifuniro chao, kapena kutopetsa maso a amasiye, kapena kudya nthongo yanga ndekha, osadyako mwana wamasiye; (pakuti kuyambira ubwana wanga analeredwa ndi ine monga ndi atate; ndipo ndinakhala nkhoswe ya wamasiye chibadwire ine.) Ngati ndinaona wina alinkutayika wopanda chovala, kapena kuti wosowa alibe chofunda; ngati ziuno zake sizinandiyamika, ngati sanafunde ubweya wa nkhosa zanga; ngati ndinasamulira ana amasiye dzanja langa, popeza ndinaona thandizo langa kuchipata; libanthuke phewa langa paphalo, ndi dzanja langa liduke pagwangwa. Pakuti tsoka lochokera kwa Mulungu linandiopsa, ndi chifukwa cha ukulu wake sindinakhoza kanthu. Ngati ndayesa golide chiyembekezo changa, ndi kunena ndi golide woyengetsa, ndiwe chikhazikitso changa; ngati ndinakondwera popeza chuma changa nchachikulu, ndi dzanja langa lapeza zochuluka; ngati ndalambira dzuwa lilikuwala, kapena mwezi ulikuyenda monyezimira; ndi mtima wanga wakopeka m'tseri, ndi pakamwa panga padapsompsona dzanja langa; ichinso ndi mphulupulu yoyenera oweruza kunena mlandu wake; pakuti ndikadakana Mulungu ali m'mwamba. Ngati ndakondwera nalo tsoka la wondida, kapena kudzitukula pompeza choipa; ndithu sindinalola m'kamwa mwanga muchimwe, kupempha motemberera moyo wake. Ngati amuna a m'hema mwanga sanati, ndani adzapeza munthu wosakhuta nyama yomgawira Yobu? Mlendo sakagona pakhwalala, koma ndinatsegulira wam'njira pakhomo panga. Ngati ndakwirira zolakwa zanga monga Adamu, ndi kubisa mphulupulu yanga m'chifuwa mwanga; popeza ndinaopa unyinji waukulu, ndi chipepulo cha mafuko chinandiopsetsa; potero ndinakhala chete osatuluka pakhomo panga. Ha! Ndikadakhala naye wina wakundimvera, chizindikiro changa sichi, Wamphamvuyonse andiyankhe; mwenzi ntakhala nao mau akundineneza analemberawo mdani wanga! Ndithu ndikadawasenza paphewa panga, ndi kudzimangirira awa ngati korona. Ndikadamfotokozera chiwerengo cha mopondamo mwanga, ndikadamsenderera Iye ngati kalonga. Ngati minda yanga ifuula monditsutsa, ndi nthumbira zake zilira pamodzi; ngati ndadya zipatso zake wopanda ndalama. Kapena kutayitsa eni ake moyo wao; imere minga m'malo mwa tirigu, ndi dawi m'malo mwa barele. Mau a Yobu atha. Pamenepo amuna atatuwa analeka kumyankha Yobu; pakuti anali wolungama pamaso pake pa iye mwini. Ndipo adapsa mtima Elihu mwana wa Barakele wa ku Buzi, wa chibale cha Ramu, adapsa mtima pa Yobu; pakuti anadziyesera yekha wolungama, wosati Mulungu. Adapsa mtima pa mabwenzi ake atatu omwe, pakuti anasowa pomyankha; koma anamtsutsa Yobu kuti ali woipa. Ndipo Elihu analindira kulankhula ndi Yobu, popeza akulu misinkhu ndi iwowa. Koma pakuona Elihu kuti anthu atatuwa anasowa poyankha pakamwa pao anapsa mtima. Ndipo Elihu mwana wa Barakele wa ku Buzi anayankha, nati, Ine ndine mnyamata, inu ndinu okalamba; chifukwa chake ndinadziletsa, ndi kuopa kukuonetsani monga umo ndayesera ine. Ndinati, Amisinkhu anene, ndi a zaka zochuluka alangize nzeru. Koma m'munthu muli mzimu, ndi mpweya wa Wamphamvuyonse wawazindikiritsa. Akulu sindiwo eni nzeru, ndi okalamba sindiwo ozindikira chiweruzo. Chifukwa chake ndinati, Ndimvereni ine, inenso ndidzaonetsa monga umo ndayesera ine. Taonani, ndinalindira mau anu, ndinatcherera khutu zifukwa zanu, pofunafuna inu ponena. Inde ndinasamalira inu; koma taonani, panalibe womtsutsa Yobu, kapena wakumbwezera mau pakati pa inu. Msamati, Tapeza nzeru ndife, Mulungu akhoza kumkhulula, si munthu ai; popeza sanandiponyere ine mau, sindidzamyankha ndi maneno anu. Asumwa, sayankhanso, Anawathera mau. Kodi ndidzangolindira popeza sanena iwo, popeza akhala duu osayankhanso? Ndidzayankha inenso mau anga, ndidzaonetsa inenso za m'mtima mwanga. Pakuti ndadzazidwa ndi mau, ndi mzimu wa m'kati mwanga undifulumiza. Taonani, m'chifuwa mwanga muli ngati vinyo wosowa popungulira, ngati matumba atsopano akuti aphulike. Ndidzanena kuti chifundo chitsike; ndidzatsegula milomo yanga ndi kuyankha. Ndisati ndisamalire nkhope ya munthu, kapena kumtchula munthu maina omdyola nao; pakuti sindidziwa kutchula maina osyasyalika; ndikatero Mlengi wanga adzandichotsa msanga. Komatu, Yobu, mumvere maneno anga, mutcherere khutu mau anga. Taonani tsono, ndatsegula pakamwa panga, lilime langa lanena m'kamwa mwanga. Maneno anga awulula chiongoko cha mtima wanga, ndi monga umo idziwira milomo yanga idzanena zoona. Mzimu wa Mulungu unandilenga, ndi mpweya wa Wamphamvuyonse umandipatsa moyo. Ngati mukhoza, mundiyankhe; mulongosolere mau anu pamaso panga, mukonzeke. Taonani, ndikhala kwa Mulungu ngati inu; inenso ndinaumbidwa ndi dothi. Taonani, kuopsa kwanga simudzachita nako mantha; ndi ichi ndikusenzetsani sichidzakulemererani. Zedi mwanena m'makutu mwanga, ndinamvanso mau a kunena kwanu, akuti, Ndine woyera ine, wopanda kulakwa, ndine wosapalamula, ndilibe mphulupulu. Taonani, Iye apeza zifukwa zoti anditsutse nazo, andiyesa mdani wake; amanga mapazi anga m'zigologolo, ayang'anira poyenda ine ponse. Taonani, ndidzakuyankhani m'mene muli mosalungama; pakuti Mulungu ndiye wamkulu woposa munthu. Mutsutsana ndi Iye chifukwa ninji? Popeza pa zake zonse sawulula chifukwa. Pakuti Mulungu alankhula kamodzi, kapena kawiri, koma anthu sasamalira. M'kulota, m'masomphenya a usiku, pakuwagwera anthu tulo tatikulu, pogona mwatcheru pakama, pamenepo atsegula makutu a anthu, nakomera chizindikiro chilangizo chao; kuti achotse munthu ku chimene akadachita, ndi kubisira munthu kudzikuza kwake; kuti amletse angaonongeke, ndi moyo wake ungatayike ndi lupanga. Alangidwanso ndi zowawa pakama pake, ndi kulimbana kowawa kosapuma m'mafupa ake. M'mwemo mtima wake uchita mseru ndi mkate, ndi moyo wake pa chakudya cholongosoka. Mnofu wake udatha, kuti sungapenyeke; ndi mafupa ake akusaoneka atuluka. Inde wasendera kufupi kumanda, ndi moyo wake kwa akuononga. Akakhala kwa iye mthenga, womasulira mau mmodzi mwa chikwi, kuonetsera munthu chomuyenera; pamenepo Mulungu amchitira chifundo, nati, Mlanditse, angatsikire kumanda, Ndampezera dipo. Mnofu wake udzakhala see, woposa wa mwana; adzabwerera kumasiku a ubwana wake. Apembedza Mulungu, ndipo amkomera mtima; m'mwemo aona nkhope yake mokondwera; ndipo ambwezera munthu chilungamo chake. Apenyerera anthu, ndi kuti, ndinachimwa, ndaipsa choongokacho, ndipo sindinapindula nako. Koma anandiombola ndingatsikire kumanda, ndi moyo wanga udzaona kuunika. Taona, izi zonse azichita Mulungu kawiri katatu ndi munthu, kumbweza angalowe kumanda, kuti kuunika kwa moyo kumuwalire. Tcherani khutu, Yobu, mundimvere ine; mukhale chete, ndipo ndidzanena ine. Ngati muli nao mau mundiyankhe. Nenani, pakuti ndifuna kukulungamitsani. Ngati mulibe mau, tamverani ine; mukhale chete, ndipo ndidzakuphunzitsani nzeru. Ndipo Elihu anabwereza kunena, nati, Tamverani mau anga, inu anzeru; munditcherere khutu inu akudziwa. Pakuti khutu liyesa mau, monga m'kamwa mulawa chakudya. Tidzisankhire choyeneracho, tidziwe mwa tokha chokomacho. Pakuti Yobu wanena, Ine ndine wolungama, ndipo Mulungu wandichotsera choyenera ine Kodi ndidzinamizire? Bala langa nlosapola, ngakhale sindinalakwa. Wakunga Yobu ndani, wakumwa mwano ngati madzi? Wakutsagana nao ochita mphulupulu, nayendayenda nao anthu oipa. Pakuti anati, Munthu sapindula kanthu nako kuvomerezana naye Mulungu. Chifukwa chake mundimvere ine, eni nzeru inu, nkutali ndi Mulungu kuchita choipa, ndi Wamphamvuyonse kuchita chosalungama. Pakuti ambwezera munthu monga mwa ntchito yake, napezetsa munthu aliyense monga mwa mayendedwe ake. Ndithu zoonadi, Mulungu sangachite choipa, ndi Wamphamvuyonse sangaipse mlandu. Anamuikiza dziko lapansi ndani? Kapena anakonzeratu dziko lonse lokhalamo anthu ndani? Akadzikumbukira yekha mumtima mwake, akadzisonkhanitsira yekha mzimu wake ndi mpweya wake, zamoyo zonse zidzatsirizika pamodzi, ndi munthu adzabwerera kufumbi. Ngati tsono uli nako kuzindikira, tamvera ichi, Tcherera khutu kunena kwanga. Kodi munthu woipidwa nacho chiweruzo adzalamulira? Ndipo kodi utsutsa wolungama ndi wamphamvuyo kuti ngwoipa? Kodi kuyenera kunena kwa mfumu, Wopanda pake iwe, kapena kwa akalonga, Oipa inu? Nanga kwa Iye wosasamalira nkhope za akalonga, wosasiyanitsa pakati pa wolemera ndi wosauka? Pakuti onsewo ndiwo ntchito ya manja ake. M'kamphindi akufa, ngakhale pakati pa usiku, anthu agwedezeka, napita, amphamvu achotsedwa opanda dzanja lakuwachotsa. Pakuti maso ake ali pa njira ya munthu aliyense, napenya moponda mwake monse. Palibe mdima kapena mthunzi wa imfa, kuti ochita zopanda pake abisaleko. Pakuti Mulungu alibe chifukwa cha kulingiriranso za munthu, kuti afike kwa Iye kudzaweruzidwa. Aphwanya eni mphamvu osatulutsa kubwalo mlandu wao, naika ena m'malo mwao. Pakuti asamalira ntchito zao, nawagubuduza usiku kuti aphwanyike. Awakantha ngati oipa, poyera pamaso pa anthu, popeza anapatuka, naleka kumtsata, osasamalira njira zake zilizonse. M'mwemo anafikitsa kwa Iye kufuula kwa osauka; ndipo anamva Iye kufuula kwa ozunzika. Iye akapatsa mpumulo adzamtsutsa ndani? Akabisa nkhope yake adzampenyerera ndani? Chikachitika pa mtundu wa anthu, kapena pa munthu, nchimodzimodzi; kuti munthu wonyoza Mulungu asachite ufumu, ndi anthu asakodwe mumsampha. Pakuti pali wina kodi anati kwa Mulungu, ndasenza kulanga kwanu, ndingakhale sindinalakwa? Chimene sindichiona mundilangize ndi Inu, ngati ndachita chosalungama sindidzabwerezanso. Kodi chilango cha Mulungu chikhale monga muchifuna inu, pakuti muchikana? Musankhe ndi inu, ine ai; m'mwemo monga mudziwa, nenani. Anthu ozindikira adzanena nane, inde anthu anzeru onse akundimva adzati, Yobu alankhula wopanda kudziwa, ndi mau ake alibe nzeru. Mwenzi nayesedwe Yobu kufikira kutha, chifukwa cha kuyankha kwake monga anthu amphulupulu. Pakuti pa kuchimwa kwake aonjeza kupikisana ndi Mulungu, asansa manja pakati pa ife, nachulukitsa maneno ake pa Mulungu. Ndipo Elihu anabwereza kunena, nati, Kodi muchiyesa choyenera, umo mukuti, Chilungamo changa chiposa cha Mulungu, pakuti munena, Upindulanji nacho? Posachimwa ndinapindula chiyani chimene sindikadapindula pochimwa? Ndidzakuyankhani, ndi anzanu pamodzi ndi inu. Yang'anani kumwamba, nimuone, tapenyani mitambo yokwera yakuposa inu. Ngati mwachimwa, mumchitira Iye chiyani? Zikachuluka zolakwa zanu, mumchitira Iye chiyani? Mukakhala wolungama, mumninkhapo chiyani? Kapena alandira chiyani pa dzanja lanu? Choipa chanu chikhoza kuipira munthu wonga inu, ndi chilungamo chanu chikhoza kukomera wobadwa ndi munthu. Chifukwa cha kuchuluka masautso anthu anafuula, afuula chifukwa cha dzanja la amphamvu. Koma palibe anganene, Ali kuti Mulungu Mlengi wanga, wakupatsa nyimbo usiku; wakutilangiza ife koposa nyama za padziko, wakutipatsa nzeru zoposa mbalame za m'mlengalenga? Apo afuula, koma Iye sawayankha; chifukwa cha kudzikuza kwa anthu oipa. Zedi Mulungu samvera zachabe, ndi Wamphamvuyonse sazisamalira. Inde mungakhale munena, Sindimpenya, mlanduwo uli pamaso pake, ndipo mumlindira. Ndipo tsopano popeza analibe kumzonda m'kukwiya kwake, ndi kusamalitsa cholakwa, chifukwa chake Yobu anatsegula pakamwa pake mwachabe, nachulukitsa mau opanda nzeru. Elihu anabwereza, nati, Mundilole pang'ono, ndidzakuuzani, pakuti ndili naonso mau akunenera Mulungu. Ndidzatenga nzeru zanga kutali, ndidzavomereza kuti Mlengi wanga ndi wolungama. Pakuti zoonadi, mau anga sali abodza, wakudziwitsa mwangwiro ali nanu. Taonani, Mulungu ndiye mwini mphamvu, ndipo sapeputsa munthu; mphamvu ya nzeru zake ndi yaikulu. Sasunga woipa akhale ndi moyo, koma awaninkha ozunzika zowayenera iwo. Sawachotsera wolungama maso ake, koma pamodzi ndi mafumu pa mpando wao awakhazika chikhazikire, ndipo akwezeka. Ndipo akamangidwa m'nsinga, nakakodwa ndi zingwe za mazunzo, pamenepo awafotokozera ntchito zao, ndi zolakwa zao, kuti anachita modzikuza. Awatseguliranso m'khutu mwao kuti awalangize, nawauza abwerere kuleka mphulupulu. Akamvera ndi kumtumikira, adzatsiriza masiku ao modala, ndi zaka zao mokondwera. Koma akapanda kumvera adzatayika ndi lupanga, nadzatsirizika osadziwa kanthu. Koma iwo a mtima wakunyoza Mulungu, akundika mkwiyo, akawamanga Iye, safuulira. Iwowa akufa akali biriwiri, ndi moyo wao utayika ngati odetsedwa. Apulumutsa wozunzika mwa kuzunzika kwake, nawatsegulira m'khutu mwao mwa kupsinjika kwao. Inde akadakukopani muchoke posaukira, mulowe kuchitando kopanda chopsinja; ndipo zoikidwa pagome panu zikadakhala zonona ndithu. Koma mukadzazidwa nazo zolingirira oipa, zolingirirazo ndi chiweruzo zidzakugwiranibe. Pakuti muchenjere, mkwiyo ungakunyengeni muchite mnyozo; ndipo usakusokeretseni ukulu wa dipoli. Chuma chanu chidzafikira kodi, kuti simudzakhala wopsinjika, kapena mphamvu yanu yonse yolimba? Musakhumbe usiku, umene anthu alikhidwe m'malo mwao. Chenjerani, musalunjike kumphulupulu; pakuti mwaisankha iyi mutazunzidwa. Taonani, Mulungu achita mokwezeka mu mphamvu yake, mphunzitsi wakunga Iye ndani? Anamuikira njira yake ndani? Adzati ndani, Mwachita chosalungama? Kumbukirani kuti mukuze ntchito zake zimene anaziimbira anthu. Anthu onse azipenyerera, anthu aziyang'anira kutali. Taonani, Mulungu ndiye wamkulu, ndipo sitimdziwa; chiwerengo cha zaka zake nchosasanthulika. Pakuti akweza madontho a mvula, akhetsa mvula ya m'nkhungu yake Imene mitambo itsanulira, nivumbitsira anthu mochuluka. Pali munthu kodi wodziwitsa mayalidwe a mitambo, ndi kugunda kwa msasa wake? Taonani, Iye ayala kuunika kwake pamenepo. Navundikira kunsi kwake kwa nyanja. Pakuti aweruza nazo mitundu ya anthu apatsa chakudya chochuluka. Akutidwa manja ake ndi mphezi, nailamulira igwere pofunapo Iye. Kugunda kwake kulalikira za Iye, zoweta zomwe zilota mtambo woyandikira. Pa ichinso mtima wanga unjenjemera, nusunthika m'malo mwake. Mvetsetsani chibumo cha mau ake, ndi kugunda kotuluka m'kamwa mwake. Akumveketsa pansi pa thambo ponse, nang'anipitsa mphezi yake ku malekezero a dziko lapansi. Mau abuma kuitsata, agunda ndi mau a ukulu wake, ndipo sailetsa atamveka mau ake. Mulungu agunda modabwitsa ndi mau ake, achita zazikulu osazidziwa ife. Pakuti anena kwa chipale chofewa, Ugwe padziko, momwemonso kwa mvula, ndi kwa mvumbi waukulu. Atsekereza mokhomera chizindikiro dzanja la munthu aliyense, kuti anthu onse anawalenga adziwe. Pamenepo zilombo zilowa mobisalamo, nizikhala m'ngaka mwao. M'chipinda mwake mutuluka kamvulumvulu, ndi chisanu chifuma kumpoto. Mwa kupuma kwake Mulungu apereka chipale, ndi madzi achitando aundana. Asenzetsanso mtambo wakuda bii madzi, afunyulula mtambo wokhalamo mphezi yake; ndipo utembenukatembenuka pakulangiza kwake, kuti uchite zilizonse aulamulira, pa nkhope ya dziko lokhalamo anthu; ngati aufikitsira dziko lake kulidzudzula, kapena kulichitira chifundo. Tamverani ichi, Yobu. Taimani, mulingirire zodabwitsa za Mulungu. Kodi mudziwa umo Mulungu azilangizira zimenezi, nawalitsa mphezi ya m'mtambo mwake? Kodi mudziwa madendekeredwe ake a mitambo, zodabwitsa za Iye wakudziwa mwangwiro? Kodi mudziwa umo zovala zanu zifundira, pamene dziko lili thuu chifukwa cha mwera? Kodi muyala thambo pamodzi ndi Iye, ndilo lolimba ngati kalirole woyengeka? Mutilangize chimene tidzanena ndi Iye; sitidziwa kulongosola mau athu chifukwa cha mdima. Kodi munthu ayenera kumuuza kuti ndifuna kunena, kapena kodi munthu adzakhumba kumezedwa? Ndipo tsopano anthu sakhoza kupenyerera kuunika pakunyezimira kuthambo, ndi mphepo yapita ndi kuuyeretsa. Kuchokera kumpoto kudzera kuwala konyezimira, Mulungu ali nao ukulu woopsa. Kunena za Wamphamvuyonse, sitingamsanthule; ndiye wa mphamvu yoposa; koma mwa chiweruzo ndi chilungamo chochuluka samasautsa. M'mwemo anthu amuopa, Iye sasamalira aliyense wanzeru mumtima. Pamenepo Yehova anayankha Yobu m'kamvulumvulu, nati, Ndani uyu adetsa uphungu, ndi mau opanda nzeru? Udzimangire m'chuuno tsono ngati mwamuna; ndikufunsa, undidziwitse. Unali kuti muja ndinaika maziko a dziko lapansi? Fotokoza ngati udziwa kuzindikira. Analemba malire ake ndani, popeza udziwa? Anayesapo chingwe chake ndani? Maziko ake anakumbidwa pa chiyani? Kapena anaika ndani mwala wake wa pangodya, muja nyenyezi za m'mawa zinaimba limodzi mokondwera, ndi ana onse a Mulungu anafuula ndi chimwemwe? Kapena anatseka nyanja ndani ndi zitseko, muja idakamula ngati kutuluka m'mimba, muja ndinayesa mtambo chovala chake, ndi mdima wa bii nsalu yake yokulunga, ndi kuilembera malire anga, ndi kuika mipikizo ndi zitseko, ndi kuti, Ufike mpaka apa, osapitirirapo; apa adzaletseka mafunde ako odzikuza? Kodi walamulira m'mawa chiyambire masiku ako, ndi kudziwitsa mbandakucha malo ake; kuti agwire malekezero a dziko lapansi, nakutumule oipa achokeko? Lisandulika ngati dothi lonyata pansi pa chosindikiza, ndi zonse zibuka ngati chovala; ndi kuunika kwa oipa kuletsedwa kuti asakuone, ndi dzanja losamulidwa lithyoledwa. Kodi unalowa magwero a nyanja? Kodi unayendayenda pozama penipeni? Kodi zipata za imfa zinavumbulukira iwe? Kapena kodi unaona zipata za mthunzi wa imfa? Kodi unazindikira chitando cha dziko lapansi? Fotokozera, ngati uchidziwa chonse. Ili kuti njira yomukira pokhala kuunika? Ndi mdima, pokhala pake pali kuti, kuti upite nao kumalire ake, kuti uzindikire miseu ya kunyumba yake? Udziwa, pakuti unabadwa pamenepo, ndi masiku ako achuluka kuwerenga kwao. Kodi unalowa m'zosungiramo chipale chofewa? Kapena unapenya zosungiramo matalala, amene ndiwasungira tsiku la nsautso, tsiku lakulimbana nkhondo? Njira ili kuti yomukira pogawikana kuunika, kapena pomwazikira mphepo ya kum'mawa pa dziko lapansi? Ndani anachikumbira mchera chimvula, kapena njira ya bingu la mphezi, kuvumbitsa mvula pa dziko lopanda anthu, kuchipululu kosakhala munthu, kukhutitsa thengo la kunkhwangwala, ndi kuphukitsa msipu? Kodi mvula ili naye atate? Kapena wabala ndani madontho a mame? Chipale chinatuluka m'mimba ya yani? Ndi chisanu chochokera m'mwamba anachibala ndani? Madzi aundana ngati mwala, ndi pamwamba pa nyanja yozama mpogwirana madzi. Kodi ungamange gulu la Nsangwe? Kapena kumasula zomangira za Akamwiniatsatana? Ungatulutse kodi nyenyezi m'nyengo zao monga mwa malongosoledwe ao? Kapena kutsogolera Mlalang'amba ndi ana ake? Kodi udziwa malemba a kuthambo? Ukhoza kukhazikitsa ufumu wao pa dziko lapansi? Kodi udziwa kukwezera mau ako kumitambo, kuti madzi ochuluka akukute? Kodi ukhoza kutumiza mphezi kuti zimuke, ndi kunena nawe, Tili pano? Ndani analonga nzeru m'mitambomo? Ndani waninkha nyenyezi yotsotsoka luntha? Adziwa ndani kuwerenga mitambo mwanzeru, ndi kutsanulira michenje ya kuthambo ndani, pokandika fumbi, ndi kuundana zibuma pamodzi? Kodi ukhoza kusakira mkango waukazi nyama? Ndi kukwaniritsa chakudya cha misona, pamene ibwatama m'ngaka mwao, nikhala mobisala kulaliramo? Amkonzeratu khungubwi chakudya chake ndani, pamenepo ana ake afuulira kwa Mulungu, naulukauluka osowa chakudya? Kodi udziwa nyengo yakuswana zinkhoma? Kodi wapenyerera pakuswa mbawala? Ukhoza kodi kuwerenga miyezi yakuzipitira, kapena udziwa nyengo yoti ziswane? Zithuntha, ziswa, zitaya zowawa zao. Ana ao akhala ojincha, akulira kuthengo, achoka osabwerera kwa amao. Ndani walola mbidzi ituluke yaufulu? Anaimasulira mbidzi nsinga zake ndani, imene ndachiyesa chipululu nyumba yake, ndi dziko lakhulo pokhala pake? Aseka phokoso la kumudzi, osamva kukuwa kwa wofulumiza nyama za m'goli. Poyenda ponse pamapiri mpa busa pake; ilondola chachiwisi chilichonse. Kodi njati idzavomera kukutumikira, idzakhala ku chodyetseramo chako kodi? Kodi ukhoza kumanga njati ndi lamba lake ilime m'mchera? Kapena idzakutsata kodi kufafaniza nthumbira m'zigwa? Udzaikhulupirira kodi, popeza mphamvu yake njaikulu? Udzaisiyira ntchito yako kodi? Kodi udzaitama kuti itute mbeu zako, ndi kuzisonkhanitsira kudwale? Phiko la nthiwatiwa likondwera, koma mapiko ndi nthenga zake nzofatsa kodi? Pakuti isiya mazira ake panthaka, nimafunditsa m'fumbi, niiwala kuti phazi lingawaphwanye, kapena chilombo chingawapondereze. Iumira mtima ana ake monga ngati sali ake; idzilemetsa ndi ntchito chabe, popeza ilibe mantha; pakuti Mulungu anaimana nzeru, ndipo sanaigawire luntha. Ikafika nthawi yake, iweramuka, iseka kavalo ndi wa pamsana pake. Wampatsa kavalo mphamvu yake kodi? Wamveka pakhosi pake chenjerere chogwedezeka? Wamlumphitsa kodi ngati dzombe? Ulemerero wa kumina kwake ngwoopsa. Apalasa kuchigwa, nakondwera nayo mphamvu yake; atuluka kukomana nao eni zida. Aseka mantha osaopsedwa, osabwerera kuthawa lupanga. Phodo likuti kochokocho panthiti pake, mkondo wonyezimira ndi nthungo yomwe. Ndi kunjenjemera kwaukali aimeza nthaka, osaimitsika pomveka lipenga. Pomveka lipenga akuti, Hee! Anunkhiza nkhondo ilikudza kutali, kugunda kwa akazembe ndi kuhahaza. Kodi kabawi auluka mwa nzeru zako, natambasula mapiko ake kunka kumwera? Kodi chiombankhanga chikwera m'mwamba pochilamulira iwe, nichimanga chisanja chake m'mwamba? Kwao nku thanthwe, chigona komweko, pansonga pa thanthwe pokhazikikapo. Pokhala kumeneko chiyang'ana chakudya; maso ake achipenyetsetsa chili kutali. Ana ake akumwa mwazi, ndipo pomwe pali ophedwa, apo pali icho. Ndipo Yehova anabwereza kwa Yobu, nati, Kodi wodzudzulayo atsutsane ndi Wamphamvuyonse? Wochita makani ndi Mulungu ayankhe. Pamenepo Yobu anayankha Yehova nati, Taonani, ndakhululuka ine, ndidzakubwezerani mau otani? Ndigwira pakamwa. Ndalankhula kamodzi, koma sindidzayakha; inde kawiri, koma sindionjezanso. Ndipo Yehova anamyankha Yobu m'kamvulumvulu, nati, Dzimangire m'chuuno tsono ngati mwamuna; ndidzakufunsa, undidziwitse. Chingakhale chiweruzo changa udzachithyola kodi? Udzanditsutsa kuti ndili woipa kodi, kuti ukhale wolungama ndiwe? Kodi uli nalo dzanja ngati Ine Mulungu? Kapena ukhoza kugunda ndi mau ngati Ine? Udzikometsere tsono ndi ukulu ndi kukuzika, nuvale ulemu ndi ulemerero. Tsanulira mkwiyo wako wosefuka, nupenyerere aliyense wodzikuza ndi kumchepetsa. Upenyerere aliyense wodzikuza, numtsitse, nupondereze oipa pomwe akhala. Uwakwirire pamodzi m'fumbi, uzimange nkhope zao pobisika. Pamenepo inenso ndidzakuvomereza, kuti dzanja lakolako lamanja likupulumutsa. Tapenya tsono mvuu ndinaipanga pamodzi ndi iwe, ikudya udzu ngati ng'ombe. Tapenya tsono, mphamvu yake ili m'chuuno mwake, ndi kulimbalimba kwake kuli m'mitsempha ya m'mimba yake. Igwedeza mchira wake ngati mkungudza; mitsempha ya ntchafu zake ipotana. Mafupa ake akunga misiwe yamkuwa; ziwalo zake zikunga zitsulo zamphumphu. Iyo ndiyo chiyambi cha machitidwe a Mulungu; wakuilenga anaininkha lupanga lake. Pakuti mapiri aiphukitsira chakudya, kumene zisewera nyama zonse za kuthengo. Igona pansi patsinde pa mitengo yamthunzi, pobisala pabango ndi pathawale. Mitengo yamthunzi iiphimba ndi mthunzi wao, misondodzi ya kumtsinje iizinga. Taona madzi a mumtsinje akakula, siinjenjemera; ilimbika mtima, ngakhale Yordani atupa mpaka pakamwa pake. Ikakhala maso, munthu adzaigwira kodi? Kapena kuboola m'mphuno mwake ili m'khwekhwe? Kodi ukhoza kukoka Leviyatani ndi mbedza? Kapena kukanikiza kalandira wake ndi chingwe? Kodi ukhoza kumanga m'mphuno ndi mlulu? Kapena kuboola nsagwada wake ndi mbedza? Kodi idzachulukitsa mau akukupembedza? Kapena idzanena nawe mau ofatsa? Kodi idzapangana ndi iwe, kuti uitenge ikhale kapolo wako wachikhalire? Kodi udzasewera nayo ngati mbalame? Kapena udzaimangira anamwali ako kuti aiwete? Kodi opangana malonda adzaitsatsa? Adzaigawana eni malonda? Kodi udzadzaza khungu lake ndi ntchetho, kapena mutu wake ndi miomba? Isanjike dzanja lako; ukakumbukira nkhondoyi, sudzateronso. Taona, chiyembekezo chako cha pa iyo chipita pachabe. Kodi sadzatenga nkhawa munthu pakungoiona? Palibe wolimba mtima kuti adzaiputa. Ndipo ndaniyo adzaima pamaso pa Ine? Ndaniyo anayamba kundipatsa Ine kuti ndimthokoze? Zilizonse pansi pa thambo ponse ndi zanga. Sindikhala chete osatchula ziwalo za ng'onayo, ndi mbiri ya mphamvu yake, ndi makonzedwe ake okoma. Ndani adzasenda chovala chake chakunja? Adzalowa ndani kumizere iwiri ya mano ake? Adzatsegula ndani zitseko za pakamwa pake? Mano ake aopsa pozungulira pao. Mamba ake olimba ndiwo kudzitama kwake; amangika pamodzi ngati okomeredwatu. Alumikizana lina ndi linzake, mphepo yosalowa pakati pao. Amamatirana lina ndi linzake, agwirana osagawanikana. Pakuyetsemula ing'anipitsa kuunika, ndi maso ake akunga zikope za m'mawa. M'kamwa mwake mutuluka miuni, mbaliwali za moto zibukamo. M'mphuno mwake mutuluka utsi, ngati nkhali yobwadamuka ndi moto wa zinyatsi mpweya wake uyatsa makala, ndi m'kamwa mwake mutuluka lawi la moto. Kukhosi kwake kukhala mphamvu, ndi mantha avumbuluka patsogolo pake. Nyama yake yopsapsala igwirana ikwima pathupi pake yosagwedezeka. Mtima wake ulimba ngati mwala, inde ulimba ngati mwala wa mphero. Ikanyamuka, amphamvu achita mantha; chifukwa cha kuopsedwa azimidwa nzeru. Munthu akaiyamba ndi lupanga, ligoma; ngakhale nthungo, kapena muvi, kapena mkondo. Chitsulo ichiyesa phesi, ndi mkuwa ngati mtengo woola. Muvi suithawitsa, miyala ya pachoponyera iisandutsa chiputu. Zibonga ziyesedwa chiputu, iseka kuthikuza kwake kwa nthungo. Kumimba kwake ikunga mapale akuthwa, itasalala kuthope ngati chopunthira. Ichititsa nthubwinthubwi pozama ngati nkhali, isanduliza nyanja ikunge mafuta. Ichititsa mifunde yonyezimira pambuyo pake; munthu akadati pozama pali ndi imvi. Pa dziko lapansi palibe china cholingana nayo, cholengedwa chopanda mantha. Ipenya chilichonse chodzikuza, ndiyo mfumu ya zodzitama zonse. Pamenepo Yobu anayankha Yehova, nati, Ndidziwa kuti mukhoza kuchita zonse, ndi kuti palibe choletsa cholingirira chanu chilichonse. Ndani uyu abisa uphungu wosadziwa kanthu? Chifukwa chake ndinafotokozera zimene sindinazizindikira, zondidabwitsa, zosazidziwa ine. Tamveranitu, ndidzanena ine, ndidzakufunsani, mundidziwitse. Kumva ndidamva mbiri yanu, koma tsopano ndikupenyani maso; chifukwa chake ndekha ndidzinyansa, ndi kulapa m'fumbi ndi mapulusa. Kunali tsono atanena Yehova mau awa kwa Yobu, Yehova anati kwa Elifazi wa ku Temani, Mkwiyo wanga wakuyakira iwe ndi mabwenzi ako awiri, pakuti simunandinenera choyenera monga ananena mtumiki wanga Yobu. Ndipo tsono, mudzitengere ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri, mumuke kwa mtumiki wanga Yobu, mudzifukizire nokha nsembe yopsereza; ndi mtumiki wanga Yobu adzapempherera inu, pakuti ndidzamvomereza iyeyu, kuti ndisachite nanu monga mwa kupusa kwanu; popeza simunandinenera choyenera monga ananena mtumiki Yobu. Namuka Elifazi wa ku Temani, ndi Bilidadi Msuki, ndi Zofari wa ku Naama, nachita monga Yehova adawauza; ndipo Yehova anavomereza Yobu. Ndipo Yehova anachotsa ukapolo wa Yobu, pamene anapempherera mabwenzi ake; Yehova nachulukitsa zake zonse za Yobu mpaka kuziwirikiza. Pamenepo anamdzera abale ake onse, ndi alongo ake onse, ndi onse odziwana naye kale, nadya naye mkate m'nyumba yake, nampukusira mitu, namtonthoza pa zoipa zonse Yehova anamfikitsirazi; nampatsanso yense ndalama ndi mphete yagolide. Ndipo Yehova anadalitsa chitsiriziro cha Yobu koposa chiyambi chake, ndipo anali nazo nkhosa zikwi khumi ndi zinai, ndi ngamira zikwi zisanu ndi chimodzi, ndi ng'ombe zamagoli chikwi chimodzi, ndi abulu akazi chikwi chimodzi. Anali naonso ana amuna asanu ndi awiri ndi ana akazi atatu. Ndipo anamutcha dzina la woyamba Yemima, ndi dzina la wachiwiri Keziya, ndi dzina la wachitatu Kerenihapuki. Ndipo m'dziko monse simunapezeka akazi okongola ngati ana akazi a Yobu, nawapatsa cholowa atate wao pamodzi ndi alongo ao. Ndipo zitatha izi, Yobu anakhala ndi moyo zaka zana limodzi mphambu makumi anai, naona ana ake ndi zidzukulu zake mibadwo inai. Namwalira Yobu, wokalamba ndi wa masiku ochuluka. Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa, kapena wosaimirira m'njira ya ochimwa, kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza. Komatu m'chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m'chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku. Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo. Oipa satero ai; koma akunga mungu wouluka ndi mphepo. Chifukwa chake oipa sadzaimirira pa mlanduwo, kapena ochimwa mu msonkhano wa olungama. Pakuti Yehova adziwa mayendedwe a olungama; koma mayendedwe a oipa adzatayika. Aphokoseranji amitundu, nalingiriranji anthu zopanda pake? Adzikhazikitsa mafumu a dziko lapansi, nachita upo akulu pamodzi, Kutsutsana naye Yehova, ndi Wodzozedwa wake, ndi kuti, Tidule zomangira zao, titaye nsinga zao. Wokhala m'mwambayo adzaseka; Ambuye adzawanyoza. Pomwepo adzalankhula nao mu mkwiyo wake, nadzawaopsa m'ukali wake. Koma Ine ndadzoza mfumu yanga Pa Ziyoni, phiri langa loyera. Ndidzauza za chitsimikizo: Yehova ananena ndi Ine, Iwe ndiwe Mwana wanga; Ine lero ndakubala. Undifunse, ndipo ndidzakupatsa amitundu akhale cholowa chako, ndi malekezero a dziko lapansi akhale akoako. Udzawathyola ndi ndodo yachitsulo; udzawaphwanya monga mbiya ya woumba. Tsono, mafumu inu, chitani mwanzeru; langikani, oweruza inu a dziko lapansi. Tumikirani Yehova ndi mantha, ndipo kondwerani ndi chinthenthe. Mpsompsoneni Mwanayo, kuti angakwiye, ndipo mungatayike m'njira ukayaka pang'ono pokha mkwiyo wake. Odala onse akumkhulupirira Iye. Salimo la Davide, muja anathawa Abisalomu mwana wake. Yehova! Ha! Achuluka nanga akundisautsa ine! Akundiukira ine ndi ambiri. Ambiri amati kwa moyo wanga, alibe chipulumutso mwa Mulungu. Ndipo Inu Yehova, ndinu chikopa changa; ulemerero wanga, ndi wondiweramutsa mutu wanga. Ndifuula kwa Yehova ndi mau anga, ndipo andiyankha m'phiri lake loyera. Ndinagona ine pansi, ndinagona tulo; ndinauka; pakuti Yehova anandichirikiza. Sindidzaopa unyinji wa anthu akundizinga ine. Ukani Yehova; ndipulumutseni, Mulungu wanga! Pakuti mwapanda adani anga onse patsaya; mwawathyola mano oipawo. Chipulumutso ncha Yehova; dalitso lanu likhale pa anthu anu. Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Neginoto. Salimo la Davide. Pakufuula ine mundiyankhe, Mulungu wa chilungamo changa; pondichepera mwandikulitsira malo. Ndichitireni chifundo, imvani pemphero langa. Amuna inu, ulemu wanga udzakhala wamanyazi kufikira liti? Mudzakonda zachabe, ndi kufunafuna bodza kufikira liti? Koma dziwani kuti Yehova anadzipatulira yekha womkondayo, adzamva Yehova m'mene ndimfuulira Iye. Chitani chinthenthe, ndipo musachimwe. Nenani mumtima mwanu pakama panu, ndipo mukhale chete. Iphani nsembe za chilungamo, ndipo mumkhulupirire Yehova. Ambiri amati, Adzationetsa chabwino ndani? Weramutsirani ife kuunika kwa nkhope yanu, Yehova. Mwapatsa chimwemwe mumtima mwanga, chakuposa chao m'nyengo yakuchuluka dzinthu zao ndi vinyo wao. Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo; chifukwa Inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino. Kwa Mkulu wa Nyimbo; aimbire zitoliro. Salimo la Davide. Mverani mau anga, Yehova, Zindikirani kulingirira kwanga. Tamvetsani mau a kufuula kwanga, Mfumu yanga, ndi Mulungu wanga; pakuti kwa Inu ndimapemphera. M'mawa, Yehova, mudzamva mau anga; m'mawa, ndidzakukonzerani pemphero langa, ndipo ndidzadikira. Pakuti Inu sindinu Mulungu wakukondwera nacho choipa mphulupulu siikhala ndi Inu. Opusa sadzakhazikika pamaso panu, mudana nao onse akuchita zopanda pake. Mudzaononga iwo akunena bodza; munthu wokhetsa mwazi ndi wachinyengo, Yehova anyansidwa naye. Koma ine, mwa kuchuluka kwa chifundo chanu ndidzalowa m'nyumba yanu; ndidzagwada kuyang'ana Kachisi wanu woyera ndi kuopa Inu. Yehova, munditsogolere m'chilungamo chanu, chifukwa cha akundizondawo; mulungamitse njira yanu pamaso panga. Pakuti m'kamwa mwao mulibe mau okhazikika; m'kati mwao m'mosakaza; m'mero mwao ndi manda apululu; lilime lao asyasyalika nalo. Muwayese otsutsika Mulungu; agwe nao uphungu wao. M'kuchuluka kwa zolakwa zao muwapirikitse; pakuti anapikisana ndi Inu. Koma akondwere onse amene athawira kwa Inu, afuule mokondwera kosaleka, popeza muwafungatira; nasekere mwa Inu iwo akukonda dzina lanu. Pakuti Inu, Yehova, mudzadalitsa wolungamayo; mudzamtchinjiriza nacho chivomerezo ngati chikopa. Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Neginoto, pa Seminiti. Salimo la Davide. Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu, ndipo musandilange m'kukali wanu. Mundichitire chifundo, Yehova; pakuti ndalefuka ine. Mundichize, Yehova; pakuti anthunthumira mafupa anga. Moyo wanganso wanthunthumira kwakukulu; ndipo Inu, Yehova, kufikira liti? Bwererani Yehova, landitsani moyo wanga; ndipulumutseni chifukwa cha kukoma mtima kwanu. Pakuti muimfa m'mosakumbukira Inu; m'mandamo adzakuyamikani ndani? Ndalema nako kuusa moyo kwanga; ndiyandamitsa kama wanga usiku wonse; mphasa yanga ndiolobza ndi misozi yanga. Lapuwala diso langa chifukwa cha chisoni; lakalamba chifukwa cha onse akundisautsa. Chokani kwa ine, nonsenu akuchita zopanda pake; pakuti wamva Yehova mau a kulira kwanga. Wamva Yehova kupemba kwanga; Yehova adzalandira pemphero langa. Adzachita manyazi, nadzanthunthumira kwakukulu adani anga onse; adzabwerera, nadzachita manyazi modzidzimuka. Syigayoni wa Davide woimbira Yehova, chifukwa cha mau a Kusi Mbenjamini. Yehova Mulungu wanga, ndakhulupirira Inu; mundipulumutse kwa onse akundilonda, nimundilanditse; kuti angamwetule moyo wanga ngati mkango, ndi kuukadzula, wopanda wina wondilanditsa. Yehova Mulungu wanga, ngati ndachita ichi; ngati m'manja anga muli chosalungama; ngati ndambwezera choipa iye woyanjana ndine; (inde, ndamlanditsa wondisautsa kopanda chifukwa); mdani alondole moyo wanga, naupeze; naupondereze pansi moyo wanga, naukhalitse ulemu wanga m'fumbi. Ukani Yehova mu mkwiyo wanu, nyamukani chifukwa cha ukali wa akundisautsa; ndipo mugalamukire ine; mwalamulira chiweruzo. Ndipo ukuzingeni msonkhano wa anthu; ndipo pamwamba pao mubwerere kunka kumwamba. Yehova aweruza anthu mlandu; mundiweruze, Yehova, monga mwa chilungamo changa, ndi ungwiro wanga uli mwa ine. Ithe mphulupulu ya anthu oipa, ndikupemphani, koma wolungamayo mumkhazikitse. Pakuti woyesa mitima ndi impso ndiye Mulungu wolungama. Chikopa changa chili ndi Mulungu, wopulumutsa oongoka mtima. Mulungu ndiye Woweruza wolungama, ndiye Mulungu wakukwiya masiku onse. Akapanda kutembenuka munthu, iye adzanola lupanga lake; wakoka uta wake, naupiringidza. Ndipo anamkonzera zida za imfa; mivi yake aipanga ikhale yansakali. Taonani, ali m'chikuta cha zopanda pake; anaima ndi chovuta, nabala bodza. Anachita dzenje, nalikumba, nagwa m'mbuna yomwe anaikumba. Chovuta chake chidzambwerera mwini, ndi chiwawa chake chidzamgwera pakati pamutu pake. Ndidzayamika Yehova monga mwa chilungamo chake; ndipo ndidzaimbira Yehova Wam'mwambamwamba. Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Gititi. Salimo la Davide. Yehova, Ambuye wathu, dzina lanu liposadi nanga pa dziko lonse lapansi! Inu amene munaika ulemerero wanu pa thambo la kumwamba. M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munakhazikitsa mphamvu, chifukwa cha otsutsana ndi Inu, kuti muwaletse mdani ndi wobwezera chilango. Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika, munthu ndani kuti mumkumbukira? Ndi mwana wa munthu kuti mucheza naye? Pakuti munamchepsa pang'ono ndi Mulungu, munamveka iye korona wa ulemerero ndi ulemu. Munamchititsa ufumu pa ntchito za manja anu; mudagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake; nkhosa ndi ng'ombe, zonsezo, ndi nyama za kuthengo zomwe; mbalame za m'mlengalenga, ndi nsomba za m'nyanja. Zopita m'njira za m'nyanja. Yehova, Ambuye wathu, dzina lanu liposadi nanga pa dziko lonse lapansi! Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Muti-Labeni. Salimo la Davide. Ndidzayamika Yehova ndi mtima wanga wonse; ndidzawerengera zodabwitsa zanu zonse. Ndidzakondwerera ndi kusekera mwa Inu; ndidzaimbira dzina lanu, Wam'mwambamwamba Inu. Pobwerera m'mbuyo adani anga, akhumudwa naonongeka pankhope panu. Pakuti mwandiweruzira mlandu wanga; mwakhala pa mpando wachifumu, woweruza wolungama. Mwadzudzula amitundu, mwaononga woipayo, mwafafaniza dzina lao kunthawi yonka muyaya. Adaniwo atha psiti, apululuka nthawi zonse; ndipo midziyo mwaipasula, chikumbukiro chao pamodzi chatha. Koma Yehova akhala chikhalire, anakonzeratu mpando wachifumu wake kuti aweruze. Ndipo Iyeyu adzaweruza dziko lapansi m'chilungamo, nadzaweruza anthu molunjika. Ndipo Yehova adzakhala msanje kwa iye wokhalira mphanthi. Msanje m'nyengo za nsautso; ndipo iwo akudziwa dzina lanu adzakhulupirira Inu; pakuti, Inu Yehova, simunawasiya iwo akufuna Inu. Imbirani zoyamika Yehova, wokhala ku Ziyoni; lalikirani mwa anthu ntchito zake. Pakuti Iye wofuna chamwazi awakumbukira; saiwala kulira kwa ozunzika. Ndichitireni chifundo, Yehova; penyani kuzunzika kwanga kumene andichitira ondidawo, inu wondinyamula kundichotsa kuzipata za imfa. Kuti ndibukitse lemekezo lanu lonse; pa bwalo la mwana wamkazi wa Ziyoni, ndidzakondwera nacho chipulumutso chanu. Amitundu anagwa m'mbuna imene anaikumba, lakodwa phazi lao muukonde anautcha. Anadziwika Yehova, anachita kuweruza, woipayo anakodwa ndi ntchito ya manja ake. Oipawo adzabwerera kumanda, inde amitundu onse akuiwala Mulungu. Pakuti sadzaiwalika nthawi zonse waumphawi, kapena chiyembekezo cha ozunzika sichidzaonongeka kosatha. Ukani, Yehova, asalimbike munthu; amitundu aweruzidwe pankhope panu. Muwachititse mantha, Yehova; adziwe amitundu kuti ali anthu. Muimiranji patali, Yehova? Mubisaliranji m'nyengo za nsautso? Podzikuza woipa apsereza waumphawi; agwe m'chiwembu anapanganacho. Pakuti woipa adzitamira chifuniro cha moyo wake, adalitsa wosirira, koma anyoza Yehova. Woipa, monga mwa kudzikuza kwa nkhope yake, akuti, Sadzafunsira. Malingaliro ake onse akuti, Palibe Mulungu. Mayendedwe ake alimbika nthawi zonse; maweruzo anu ali pamwamba posaona iye; adani ake onse awanyodola. Ati mumtima mwake, Sindidzagwedezeka ine; ku mibadwomibadwo osagwa m'tsoka ine. M'kamwa mwake mwadzala kutemberera ndi manyengo ndi kuchenjerera; pansi pa lilime lake pali chivutitso chopanda pake. Akhala m'molalira midzi; mobisalamo akupha munthu wosachimwa. Ambisira waumphawi nkhope yake. Alalira monga mkango m'ngaka mwake; alalira kugwira wozunzika, agwira wozunzika, pakumkola m'ukonde mwake. Aunthama, nawerama, ndipo aumphawi agwa m'zala zake. Anena m'mtima mwake, Mulungu waiwala; wabisa nkhope yake; sapenya nthawi zonse. Ukani, Yehova; samulani dzanja lanu, Mulungu; musaiwale ozunzika. Woipa anyozeranji Mulungu, anena m'mtima mwake, Simudzafunsira? Mwapenya; pakuti mumayang'anira chivutitso ndi chisoni kuti achipereke m'manja mwanu; waumphawi adzipereka kwa Inu; wamasiye mumakhala mthandizi wake. Thyolani mkono wa woipa; ndipo wochimwa, mutsate choipa chake kufikira simuchipezanso china. Yehova ndiye Mfumu kunthawi yamuyaya; aonongeka amitundu m'dziko lake. Yehova, mwamva chikhumbo cha ozunzika, mudzakhazikitsa mtima wao, mudzatchereza khutu lanu; kuti muweruze mlandu wa amasiye ndi wokhalira mphanthi, kuti munthu wa pa dziko lapansi angaonjeze kuopsa. Kwa Mkulu wa Nyimbo; Salimo la Davide. Ndakhulupirira Yehova, mutani nkunena kwa moyo wanga, Thawirani kuphiri lanu ngati mbalame? Pakuti, onani, oipa akoka uta, apiringidza muvi wao pansinga, kuwaponyera mumdima oongoka mtima. Akapasuka maziko, wolungama angachitenji? Yehova ali m'Kachisi wake woyera, Yehova, mpando wachifumu wake uli m'Mwamba; apenyerera ndi maso ake, ayesa ana a anthu ndi zikope zake. Yehova ayesa wolungama mtima, koma moyo wake umuda woipa ndi iye wakukonda chiwawa. Adzagwetsa pwatapwata misampha pa oipa; moto ndi miyala ya sulufure, ndi mphepo yoopsa zidzawagawikira m'chikho chao. Pakuti Yehova ndiye wolungama; akonda zolungama; woongoka mtima adzapenya nkhope yake. Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Seminiti. Salimo la Davide. Pulumutsani, Yehova; pakuti wofatsa wasowa; pakuti okhulupirika achepa mwa ana a anthu. Amanena za bodza munthu yense ndi mnansi wake, amanena ndi mlomo wothyasika, ndi mitima iwiri. Yehova adzadula milomo yonse yothyasika, lilime lakudzitamandira; amene amati, Ndi lilime lathu tidzaposa; milomo yathu nja ife eni; mbuye wa pa ife ndani? Chifukwa cha kupasuka kwa ozunzika, chifukwa cha kuusa moyo kwa aumphawi, ndiuka tsopano, ati Yehova; ndidzamlonga mosungika muja alakalakamo. Mau a Yehova ndi mau oona; ngati siliva woyenga m'ng'anjo yadothi, yoiyeretsa kasanu ndi kawiri. Mudzawasunga, Yehova, mudzawatchinjirizira mbadwo uno kunthawi zonse. Oipa amayenda mozungulirazungulira, potamanda iwo chonyansa mwa ana a anthu. Kwa Mkulu wa Nyimbo; Salimo la Davide. Mudzandiiwala chiiwalire, Yehova, kufikira liti? Mudzandibisira ine nkhope yanu kufikira liti? Ndidzachita uphungu m'moyo mwanga kufikira liti, pokhala ndi chisoni m'mtima mwanga tsiku lonse? Adzandiukira ine mdani wanga kufikira liti? Penyani, ndiyankheni, Yehova Mulungu wanga. Penyetsani maso anga, kuti ndingagone tulo ta imfa; kuti anganene mdani wanga, Ndamlaka; ndipo angakondwere otsutsana nane posunthika ine. Koma ine ndakhulupirira pa chifundo chanu; mtima wanga udzakondwera nacho chipulumutso chanu. Ndidzaimbira Yehova, pakuti anandichitira zokoma. Kwa Mkulu wa Nyimbo; Salimo la Davide. Wauchitsiru amati mumtima mwake, Kulibe Mulungu. Achita zovunda, achita ntchito zonyansa; kulibe wakuchita bwino. Yehova m'Mwamba anaweramira pa ana a anthu, kuti aone ngati aliko wanzeru, wakufuna Mulungu. Anapatuka onse; pamodzi anavunda mtima; palibe wakuchita bwino ndi mmodzi yense. Kodi onse ochita zopanda pake sadziwa kanthu? Pakudya anthu anga monga akudya mkate, ndipo saitana pa Yehova. Pamenepa anaopaopatu, pakuti Mulungu ali mu mbadwo wa wolungama. Munyazitsa uphungu wa wozunzika, koma Yehova ndiye pothawira pake. Mwenzi chipulumutso cha Israele chitachokera ku Ziyoni! Pakubweretsa Yehova anthu ake a m'nsinga, pamenepo adzakondwera Yakobo, nadzasekera Israele. Salimo la Davide. Yehova, ndani adzagonera m'chihema mwanu? Adzagonera ndani m'phiri lanu lopatulika? Iye wakuyendayo mokwanira, nachita chilungamo, nanena zoonadi mumtima mwake. Amene sasinjirira ndi lilime lake, nachitira mnzake choipa, ndipo satola miseche pa mnansi wake. M'maso mwake munthu woonongeka anyozeka; koma awachitira ulemu akuopa Yehova. Atalumbira kwa tsoka lake, sasintha ai. Ndalama zake sakongoletsa mofuna phindu lalikulu, ndipo salandira chokometsera mlandu kutsutsa wosachimwa. Munthu wakuchita izi sadzagwedezeka kunthawi zonse. Mikitamu wa Davide. Ndisungeni ine, Mulungu: pakuti ndakhulupirira Inu. Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Ambuye wanga, ndilibe chabwino china choposa Inu. Za oyera mtima okhala pa dziko lapansi, iwo ndiwo omveka mbiri, mwa iwowo muli chikondwero changa chonse. Zidzachuluka zisoni zao za iwo otsata Mulungu wina. Sindidzathira nsembe zao zamwazi, ndipo sindidzatchula maina ao pakamwa panga. Yehova ndiye gawo la cholowa changa ndi chikho changa, ndinu wondigwirira cholandira changa. Zingwe zandigwera mondikondweretsa; inde chosiyira chokoma ndili nacho. Ndidzadalitsa Yehova, amene anandichitira uphungu, usikunso impso zanga zindilangiza. Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse; popeza ali pa dzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka. Chifukwa chake wasekera mtima wanga, nukondwera ulemu wanga; mnofu wanganso udzakhala mokhazikika. Pakuti simudzasiya moyo wanga kumanda; simudzalola wokondedwa wanu avunde. Mudzandidziwitsa njira ya moyo, pankhope panu pali chimwemwe chokwanira; m'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya. Pemphero la Davide. Yehova, imvani chilungamo, mverani mfuu wanga; tcherani khutu ku pemphero langa losatuluka m'milomo ya chinyengo. Pankhope panu patuluke chiweruzo changa; maso anu apenyerere zolunjika. Mwayesera mtima wanga; mwandizonda usiku; mwandisuntha, simupeza kanthu; mwatsimikiza mtima kuti m'kamwa mwanga simudzalakwa. Za machitidwe a anthu, ndachenjera ndi mau a milomo yanu ndingalowe njira za woononga. M'mayendedwe anga ndasunga mabande anu, mapazi anga sanaterereke. Ine ndinakuitanani, pakuti mudzandiyankha, Mulungu; tcherani khutu lanu kwa ine, imvani mau anga. Onetsani chifundo chanu chodabwitsa, Inu wakupulumutsa okhulupirira Inu kwa iwo akuwaukira ndi dzanja lanu lamanja. Ndisungeni monga kamwana ka m'diso, ndifungatireni mu mthunzi wa mapiko anu, kundilanditsa kwa oipa amene andipasula, adani a pa moyo wanga amene andizinga. Mafuta ao awatsekereza; m'kamwa mwao alankhula modzikuza. Tsopano anatizinga m'mayendedwe athu, apenyetsetsa m'maso kuti atigwetse pansi. Afanana ndi mkango wofuna kumwetula, ndi msona wa mkango wakukhala mobisalamo. Ukani Yehova, Mumtsekereze, mumgwetse, landitsani moyo wanga kwa woipa ndi lupanga lanu; kwa anthu, ndi dzanja lanu, Yehova, kwa anthu a dziko lapansi pano amene cholowa chao chili m'moyo uno, ndipo mimba yao muidzaza ndi chuma chanu chobisika; akhuta mtima ndi ana, nasiyira ana amakanda zochuluka zao. Koma ine ndidzapenyerera nkhope yanu m'chilungamo, ndidzakhuta mtima ndi maonekedwe anu, pamene ndidzauka. Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide, mtumiki wa Yehova, amene ananena kwa Yehova mau a nyimbo iyi m'mene Yehova anamlanditsa m'dzanja la adani ake onse, ndi m'dzanja la Saulo: ndipo anati, Ndikukondani, Yehova, mphamvu yanga. Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye; chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga. Ndidzaitanira Yehova, woyenera kutamandika, ndipo adzandipulumutsa ine kwa adani anga. Zingwe za imfa zinandizinga, ndipo mitsinje ya zopanda pake inandiopsa. Zingwe za manda zindizinga, misampha ya imfa inandifikira ine. M'kusauka kwanga ndinaitana Yehova, ndipo ndinakuwira Mulungu wanga; mau anga anawamva m'Kachisi mwake, ndipo mkuwo wanga wa pankhope pake unalowa m'makutu mwake. Pamenepo linagwedezeka, ndi kutenthemera dziko lapansi, ndi maziko a mapiri ananjenjemera nagwedezeka, pakuti anakwiya Iyeyo. Unakwera utsi wotuluka m'mphuno mwake, ndi moto wa m'kamwa mwake unanyeka nuyakitsa makala. Ndipo Iye anaweramitsa thambo, natsika; ndipo pansi pa mapazi ake panali mdima bii. Ndipo anaberekeka pa kerubi, nauluka; nauluka msanga pa mapiko a mphepo. Anaika mdima pobisala pake, hema wake womzinga; mdima wa madzi, makongwa a kuthambo. Mwa kuchezemira kunali pamaso pake makongwa anakanganuka, matalala ndi makala amoto. Ndipo anagunda m'mwamba Yehova, ndipo Wam'mwambamwamba anamvetsa liu lake; matalala ndi makala amoto. Ndipo anatuma mivi yake nawabalalitsa; inde mphezi zaunyinji, nawamwaza. Ndipo zidaoneka zoyendamo madzi, nafukuka maziko a dziko lapansi, mwa kudzudzula kwanu, Yehova, mwa mpumo wa mpweya wa m'mphuno mwanu. Anatuma kuchokera m'mwamba, ananditenga; anandivuula m'madzi ambiri. Anandipulumutsa ine kwa mdani wanga wamphamvu, ndi kwa iwo ondida ine, pakuti anandiposa mphamvu. Anandipeza ine tsiku la tsoka langa; koma Yehova anali mchirikizo wanga. Ananditulutsanso andifikitse motakasuka; anandilanditsa, pakuti anakondwera ndi ine. Yehova anandibwezera monga mwa chilungamo changa; anandisudzula monga mwa kusisira kwa manja anga. Pakuti ndasunga njira za Yehova, ndipo sindinachitira choipa kusiyana ndi Mulungu wanga. Pakuti maweruzo ake onse anali pamaso panga, ndipo malemba ake sindinawachotsa kwa ine. Ndipo ndinakhala wangwiro ndi Iye, ndipo ndinadzisunga wosachita choipa changa. Ndimo anandisudzulira Yehova monga mwa chilungamo changa, monga mwa kusisira kwa manja anga pamaso pake. Pa wachifundo mukhala wachifundo; pa munthu wangwiro mukhala wangwiro. Pa woyera mtima mukhala woyera mtima; pa wotsutsatsutsa mukhala wotsutsana naye. Pakuti Inu muwapulumutsa anthu aumphawi; koma maso okweza muwatsitsa. Pakuti Inu muyatsa nyali yanga; Yehova, Mulungu wanga, aunikira mdima wanga. Pakuti mwa Inu ndipyola khamu la anthu; ndipo mwa Mulungu wanga ndilumphira linga. Mulungu ndiye wangwiro m'njira zake; mau a Yehova ngoyengeka; ndiye chikopa cha onse okhulupirira Iye. Pakuti Mulungu ndani wosati Yehova? Ndipo thanthwe ndani wosati Mulungu wathu? Mulungu ndiye wondizingiza mphamvu m'chuuno, nakonza njira yanga ikhale yangwiro. Alinganiza mapazi anga ngati a mbawala, nandiimitsa pamsanje panga. Aphunzitsa manja anga agwire nkhondo; kuti walifuka uta wamkuwa ndi manja anga. Ndipo mwandipatsa chikopa cha chipulumutso chanu; ndipo dzanja lamanja lanu landigwiriziza, ndipo chifatso chanu chandikuza ine. Mwandipondetsa patalipatali, sanaterereka mapazi anga. Ndidzalondola adani anga, ndi kuwapeza, ndipo sindidzabwerera asanathe psiti. Ndidzawapyoza kuti sangakhoze kuuka, adzagwa pansi pa mapazi anga. Pakuti mwandizingiza mphamvu m'chuuno ku nkhondoyo; mwandigonjetsera amene andiukira. Ndipo adani anga mwawalozetsa m'mbuyo kwa ine, kuti ndipasule ondidawo. Anafuula, koma panalibe wopulumutsa; ngakhale kwa Yehova, koma sanawavomereze. Pamenepo ndinawapera ngati fumbi la kumphepo; ndinawakhuthula ngati matope a pabwalo. Mwandipulumutsa pa zolimbana nane za anthu; mwandiika mutu wa amitundu; mtundu wa anthu sindinaudziwa udzanditumikira. Pakumva m'khutu za ine adzandimvera, alendo adzandigonjera monyenga. Alendo adzafota, nadzatuluka monjenjemera m'ngaka mwao. Yehova ngwa moyo; ndipo lidalitsike thanthwe langa; nakwezeke Mulungu wa chipulumutso changa. Ndiye Mulungu amene andibwezerera chilango, nandigonjetsera mitundu ya anthu. Andipulumutsa kwa adani anga. Inde mundikweza pa iwo akundiukira ine, mundikwatula kwa munthu wachiwawa. Chifukwa chake Yehova ndidzakuyamikani mwa amitundu, ndipo dzina lanu ndidzaliimbira. Alanditsa mfumu yake ndi chipulumutso chachikulu; nachitira chifundo wodzozedwa wake, Davide, ndi mbumba yake, kunthawi zonse. Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide. Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake. Usana ndi usana uchulukitsa mau, ndipo usiku ndi usiku uonetsa nzeru. Palibe chilankhulidwe, palibe mau; liu lao silimveka. Muyeso wao wapitirira pa dziko lonse lapansi, ndipo mau ao ku malekezero a m'dziko muli anthu. Iye anaika hema la dzuwa m'menemo, ndipo lili ngati mkwati wakutuluka m'chipinda mwake, likondwera ngati chiphona kuthamanga m'njira. Kutuluka kwake lituluka kolekezera thambo, ndipo kuzungulira kwake lifikira ku malekezero ake; ndipo kulibe kanthu kobisalira kutentha kwake. Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo; mboni za Yehova zili zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru. Malangizo a Yehova ali olungama, akukondweretsa mtima; malamulo a Yehova ali oyera, akupenyetsa maso. Kuopa Yehova kuli mbee, kwakukhalabe nthawi zonse; maweruzo a Yehova ali oona, alungama konsekonse. Ndizo zifunika koposa golide, inde, golide wambiri woyengetsa; zizuna koposa uchi ndi zakukha za zisa zake. Ndiponso kapolo wanu achenjezedwa nazo, m'kuzisunga izo muli mphotho yaikulu. Adziwitsa zolowereza zake ndani? Mundimasule kwa zolakwa zobisika. Ndiponso muletse kapolo wanu pa zodzitama; zisachite ufumu pa ine. Pamenepo ndidzakhala wangwiro, ndi wosachimwa cholakwa chachikulu. Mau a m'kamwa mwanga ndi maganizo a m'mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga. Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide. Yehova akuvomereze tsiku la nsautso; dzina la Mulungu wa Yakobo likuike pamsanje; likutumizire thandizo lotuluka m'malo oyera, ndipo likugwirizize kuchokera m'Ziyoni; likumbukire zopereka zako zonse, lilandire nsembe yako yopsereza; likupatse cha mtima wako, ndipo likwaniritse upo wako wonse. Tidzafuula mokondwera mwa chipulumutso chanu, ndipo m'dzina la Mulungu wathu tidzakweza mbendera; Yehova akwaniritse mapempho ako onse. Tsopano ndidziwa kuti Yehova apulumutsa wodzozedwa wake; adzamvomereza m'Mwamba mwake moyera ndi mphamvu ya chipulumutso cha dzanja lake lamanja. Ena atama magaleta, ndi ena akavalo; koma ife tidzatchula dzina la Yehova Mulungu wathu. Iwowa anagonjeka, nagwa; koma ife tauka, ndipo takhala chilili. Yehova, pulumutsani, mfumuyo ativomereze tsiku lakuitana ife. Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide. Yehova, adzasekera mfumu mu mphamvu yanu; adzakondwera kwakukulu m'chipulumutso chanu! Mwampatsa iye chikhumbo cha mtima wake, ndipo simunakana pempho la milomo yake. Pakuti mufika kwa iye ndi madalitso okoma; muika korona wa golide woyengetsa pamutu pake. Anakupemphani moyo, mwampatsa iye; mwamtalikitsira masiku kunthawi za nthawi. Ulemerero wake ngwaukulu mwa chipulumutso chanu; mumchitira iye ulemu ndi ukulu. Pakuti mumuikira madalitso kunthawi zonse; mumkondweretsa ndi chimwemwe pankhope panu. Pakuti mfumu akhulupirira Yehova, ndipo mwa chifundo cha Wam'mwambamwamba sadzagwedezeka iye. Dzanja lanu lidzapeza adani anu onse, dzanja lanu lamanja lidzapeza iwo akuda Inu. Mudzawaika ngati ng'anjo yamoto pa nyengo ya mkwiyo wanu. Yehova adzawatha m'kukwiya kwake, ndipo moto udzawanyeketsa. Mudzaziononga zobala zao kuzichotsa pa dziko lapansi, ndi mbeu zao mwa ana a anthu. Pakuti anakupangirani choipa, anapangana chiwembu, osakhoza kuchichita. Pakuti mudzawabweza m'mbuyo, popiringidza m'nsinga zanu pankhope pao. Kwezekani, Yehova, mu mphamvu yanu; potero tidzaimba ndi kulemekeza chilimbiko chanu. Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Ajelet Hasakara. Salimo la Davide. Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine? Mukhaliranji kutali kwa chipulumutso changa, ndi kwa mau a kubuula kwanga? Mulungu wanga, ndiitana usana, koma simuvomereza; ndipo usiku, sindikhala chete. Koma Inu ndinu woyera, wakukhala m'malemekezo a Israele. Makolo athu anakhulupirira Inu; anakhulupirira, ndipo munawalanditsa. Anafuula kwa Inu, napulumutsidwa; anakhulupirira Inu, ndipo sanachite manyazi. Koma ine ndine nyongolotsi, si munthu ai, chotonza cha anthu, ndi wonyozedwa ndi anthu. Onse akundipenya andiseka; akwenzula, apukusa mutu, nati, Adadzitengera kwa Yehova; kuti adzampulumutsa, amlanditse tsopano popeza akondwera naye. Pakuti Inu ndinu wondibadwitsa; wondikhulupiritsa pokhala ine pa bere la mai wanga. Chibadwire ine anandisiyira Inu, kuyambira kwa mai wanga Mulungu wanga ndinu. Musandikhalire kutali; pakuti nsautso ili pafupi, pakuti palibe mthandizi. Ng'ombe zamphongo zambiri zandizinga; mphongo zolimba za ku Basani zandizungulira. Andiyasamira m'kamwa mwao, ngati mkango wozomola ndi wobangula. Ndathiridwa pansi monga madzi, ndipo mafupa anga onse anaguluka. Mtima wanga ukunga sera; wasungunuka m'kati mwa matumbo anga. Mphamvu yanga yauma ngati phale; ndi lilime langa likangamira kunsaya zanga; ndipo mwandifikitsa kufumbi la imfa. Pakuti andizinga agalu, msonkhano wa oipa wanditsekereza; andiboola m'manja anga ndi m'mapazi anga. Ndikhoza kuwerenga mafupa anga onse; iwo ayang'ana nandipenyetsetsa ine. Agawana zovala zanga, nachita maere pa malaya anga. Koma Inu, Yehova, musakhale kutali; mphamvu yanga Inu, mufulumire kundithandiza. Landitsani moyo wanga kulupanga; wokondedwa wanga kumphamvu ya galu, ndipulumutseni m'kamwa mwa mkango; inde mwandiyankha ine ndili pa nyanga za njati. Ndidzalalikira dzina lanu kwa abale anga, pakati pa msonkhano ndidzakulemekezani. Inu akuopa Yehova, mumlemekeze; inu nonse mbumba ya Yakobo, mumchitire ulemu; ndipo muchite mantha ndi Iye, inu nonse mbumba ya Israele. Pakuti sanapeputsa ndipo sananyansidwe ndi zunzo la wozunzika; ndipo sanambisire nkhope yake; koma pomfuulira Iye, anamva. Lemekezo langa lidzakhala la Inu mu msonkhano waukulu, zowinda zanga ndidzazichita pamaso pa iwo akumuopa Iye. Ozunzika adzadya nadzakhuta, adzayamika Yehova iwo amene amfuna, ukhale moyo mtima wako nthawi zonse. Malekezero onse a dziko lapansi adzakumbukira nadzatembenukira kwa Yehova, ndipo mafuko onse a amitundu adzagwadira pamaso panu. Pakuti ufumuwo ngwa Yehova; Iye achita ufumu mwa amitundu. Onenepa onse a pa dziko lapansi adzadya nadzagwadira; onse akutsikira kufumbi adzawerama pamaso pake, ndi iye amene sadziwa kusunga moyo wake. Mbumba ya anthu idzamtumikira; kudzanenedwa za Ambuye ku mibadwo yakudza. Iwo adzadza nadzafotokozera chilungamo chake kwa anthu akadzabadwa, kuti Iye anachichita. Salimo la Davide. Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa. Andigonetsa kubusa lamsipu, anditsogolera kumadzi odikha. Atsitsimutsa moyo wanga; anditsogolera m'mabande a chilungamo, chifukwa cha dzina lake. Inde, ndingakhale ndiyenda m'chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzaopa choipa; pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine. Mundiyalikira gome pamaso panga m'kuona kwa adani anga; mwandidzoza mutu wanga mafuta; chikho changa chisefuka. Inde ukoma ndi chifundo zidzanditsata masiku onse a moyo wanga, ndipo ndidzakhala m'nyumba ya Yehova masiku onse. Salimo la Davide. Dziko lapansi nla Yehova ndi zodzala zake zomwe, dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhala m'mwemo. Pakuti Iye analimanga pazinyanja, nalikhazika pamadzi. Adzakwera ndani m'phiri la Yehova? Nadzaima m'malo ake oyera ndani? Woyera m'manja, ndi woona m'mtima, ndiye; iye amene sanakweze moyo wake kutsata zachabe, ndipo salumbira monyenga. Iye adzalandira dalitso kwa Yehova, ndi chilungamo kwa Mulungu wa chipulumutso chake. Uwu ndi mbadwo wa iwo akufuna Iye, iwo akufuna nkhope yanu, Mulungu wa Yakobo. Weramutsani mitu yanu, zipata inu; ndipo kwezekani inu, zitseko zosatha, kuti Mfumu ya ulemerero ilowe. Mfumu imene ya ulemerero ndani? Yehova wamphamvu ndi wolimba, Yehova wolimba kunkhondo. Weramutsani mitu yanu, zipata inu; inde weramutsani, zitseko zosatha inu, kuti Mfumu ya ulemerero ilowe. Mfumu imene ya ulemerero ndani? Yehova wa makamumakamu, ndiye Mfumu ya ulemerero. Salimo la Davide. Ndikweza moyo wanga kwa Inu, Yehova. Mulungu wanga, ndakhulupirira Inu, ndisachite manyazi; adani anga asandiseke ine. Inde, onse akuyembekezera Inu sadzachita manyazi; adzachita manyazi iwo amene achita monyenga kopanda chifukwa. Mundidziwitse njira zanu, Yehova; Mundiphunzitse mayendedwe anu. Munditsogolere m'choonadi chanu, ndipo mundiphunzitse; pakuti Inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; Inu ndikuyembekezerani tsiku lonseli. Kumbukirani, Yehova, nsoni zanu ndi chifundo chanu; pakuti izi nza kale lonse. Musakumbukire zolakwa za ubwana wanga kapena zopikisana nanu. Mundikumbukire monga mwa chifundo chanu, chifukwa cha ubwino wanu, Yehova. Yehova ndiye wabwino ndi wolunjika mtima, chifukwa chake adzaphunzitsa olakwa za njira. Adzawatsogolera ofatsa m'chiweruzo; ndipo adzaphunzitsa ofatsa njira yake. Mayendedwe onse a Yehova ndiwo chifundo ndi choonadi, kwa iwo akusunga pangano lake ndi mboni zake. Chifukwa cha dzina lanu, Yehova, ndikhululukireni kusakaza kwanga, pakuti ndiko kwakukulu. Munthuyo wakuopa Yehova ndani? Adzamlangiza iye njira adzasankheyo. Moyo wake udzakhala mokoma; ndi mbumba zake zidzalandira dziko lapansi. Chinsinsi cha Yehova chili kwa iwo akumuopa Iye; ndipo adzawadziwitsa pangano lake. Maso anga alinga kwa Yehova kosaleka; pakuti Iye adzaonjola mapazi anga m'ukonde. Cheukirani ine ndipo ndichitireni chifundo; pakuti ndili wounguluma ndi wozunzika. Masautso a mtima wanga akula, munditulutse m'zondipsinja. Penyani mazunzo anga ndi zovuta zanga; ndipo khululukirani zolakwa zanga zonse. Penyani adani anga, popeza achuluka; ndipo andida ndi udani wachiwawa. Sungani moyo wanga, ndilanditseni, ndisakhale nao manyazi, pakuti ndakhulupirira Inu. Ungwiro ndi kuongoka mtima zindisunge, pakuti ndayembekezera Inu. Ombolani Israele, Mulungu, m'masautso ake onse. Salimo la Davide. Mundiweruze, Yehova, pakuti ndayenda m'ungwiro wanga, ndipo ndakhulupirira Yehova, sindadzaterereka. Mundiyesere, Yehova, ndipo mundisunthe; yeretsani impso zanga ndi mtima wanga. Pakuti chifundo chanu chili pamaso panga; ndipo ndayenda m'choona chanu. Sindinakhala pansi ndi anthu achabe; kapena kutsagana nao anthu othyasika. Ndidana nao msonkhano wa ochimwa, ndipo sindidzakhala nao pansi ochita zoipa. Ndidzasamba manja anga mosalakwa; kuti ndizungulire guwa la nsembe lanu, Yehova; kuti ndimveketse mau a chiyamiko, ndi kulalikira ntchito zanu zonse zozizwa. Yehova, ndikonda chikhalidwe cha nyumba yanu, ndi malo akukhalamo ulemerero wanu. Musandichotsere mzimu wanga pamodzi ndi olakwa, kapena moyo wanga pamodzi ndi anthu okhetsa mwazi; amene m'manja mwao muli mphulupulu, ndi dzanja lao lamanja ladzala ndi zokometsera mlandu. Koma ine, ndidzayenda m'ungwiro wanga; mundiombole, ndipo ndichitireni chifundo. Phazi langa liponda pachidikha, m'masonkhano ndidzalemekeza Yehova. Salimo la Davide. Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani? Pondifika ine ochita zoipa kudzadya mnofu wanga, inde akundisautsa ndi adani anga, anakhumudwa iwo nagwa. Lingakhale gulu la ankhondo limanga misasa kuti andithyole, mtima wanga sungachite mantha; ingakhale nkhondo ikandiukira, inde pomweponso ndidzakhulupirira. Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova, ndidzachilondola ichi, Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa m'Kachisi wake. Chifukwa kuti pa tsiku la tsoka Iye adzandibisa mumsasa mwake, adzandibisa m'tsenjezi mwa chihema chake; pathanthwe adzandikweza. Ndipo tsopano mutu wanga udzakwezeka pamwamba pa adani anga akundizinga; ndipo ndidzapereka m'chihema mwake nsembe za kufuula mokondwera; ndidzaimba, inde, ndidzaimbira Yehova zomlemekeza. Imvani, Yehova, liu langa pofuula ine; mundichitirenso chifundo ndipo mundivomereze. Pamene munati, Funani nkhope yanga; mtima wanga unati kwa Inu. Nkhope yanu, Yehova, ndidzaifuna. Musandibisire ine nkhope yanu; musachotse kapolo wanu ndi kukwiya. Inu munakhala thandizo langa; musanditaye, ndipo musandisiye Mulungu wa chipulumutso changa. Pakuti wandisiya atate wanga ndi amai wanga, koma Yehova anditola. Mundiphunzitse njira yanu, Yehova, munditsogolere pa njira yachidikha, chifukwa cha adani anga. Musandipereke ku chifuniro cha akundisautsa, chifukwa zinandiukira mboni zonama ndi iwo akupumira zachiwawa. Ndikadapanda kukhulupirira kuti ndikaone ubwino wa Yehova m'dziko la amoyo, ndikadatani! Yembekeza Yehova, limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; inde, yembekeza Yehova. Salimo la Davide. Kwa Inu, Yehova, ndidzafuulira; thanthwe langa, musandikhalire ngati wosamva; pakuti ngati munditontholera ine, ndidzafanana nao iwo akutsikira kumanda. Mverani mau a kupemba kwanga, pamene ndilirira Inu, pamene ndikweza manja anga kuloza ponenera panu poyera. Musandikoke kundichotsa pamodzi ndi oipa, ndi ochita zopanda pake; amene alankhula zamtendere ndi anansi ao, koma mumtima mwao muli choipa. Muwapatse monga mwa ntchito zao, ndi monga mwa choipa chochita iwo; muwapatse monga mwa machitidwe a manja ao; muwabwezere zoyenera iwo. Pakuti sasamala ntchito za Yehova, kapena machitidwe a manja ake, adzawapasula, osawamanganso. Wodalitsika Yehova, Pakuti adamva mau a kupemba kwanga. Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi chikopa changa; mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza, chifukwa chake mtima wanga ukondwera kwakukulu; ndipo ndidzamyamika nayo nyimbo yanga. Yehova ndiye mphamvu yao, inde mphamvu ya chipulumutso cha wodzozedwa wake. Pulumutsani anthu anu, ndi kudalitsa cholandira chanu; muwawetenso, ndi kuwanyamula nthawi zonse. Salimo la Davide. Perekani kwa Yehova, inu ana a amphamvu, perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu. Perekani kwa Yehova ulemerero wa dzina lake, gwadirani Yehova moyera ndi mokometsetsa. Liu la Yehova lili pamadzi; Mulungu wa ulemerero agunda, ndiye Yehova pa madzi ambiri. Liu la Yehova ndi lamphamvu; liu la Yehova ndi lalikulukulu. Liu la Yehova lithyola mitengo yamkungudza; inde Yehova athyola mikungudza ya ku Lebanoni. Aitumphitsa monga mwanawang'ombe; Lebanoni ndi Sirioni monga msona wa njati. Liu la Yehova ligawa malawi a moto. Liu la Yehova ligwedeza chipululu; Yehova agwedeza chipululu cha Kadesi. Liu la Yehova liswetsa nyama zazikazi, ndipo lipulula nkhalango; ndipo m'Kachisi mwake zonse zili m'mwemo zimati, Ulemerero. Yehova anakhala pa chigumula, inde Yehova akhala mfumu kunthawi yonka muyaya. Yehova adzapatsa anthu ake mphamvu, Yehova adzadalitsa anthu ake ndi mtendere. Salimo la Davide. Nyimbo yakuperekera nyumba kwa Mulungu. Ndidzakukwezani, Yehova; pakuti mwandinyamutsa, ndipo simunandikondwetsera adani anga. Yehova, Mulungu wanga, ndinafuulira kwa Inu, ndipo munandichiritsa. Yehova munabweza moyo wanga kumanda, munandisunga ndi moyo, kuti ndingatsikire kudzenje. Imbirani Yehova, inu okondedwa ake, ndipo yamikani pokumbukira chiyero chake. Pakuti mkwiyo wake ukhala kanthawi kokha; koma kuyanja kwake moyo wonse. Kulira kuchezera, koma mamawa kuli kufuula kokondwera. Ndipo ine, ndinanena m'phindu langa, sindidzagwedezeka nthawi zonse. Inu, Yehova, munakhazikitsa phiri langa ndi kuyanja kwanu; munabisa nkhope yanu; ndinaopa. Ndinafuulira kwa Inu, Yehova; kwa Yehova ndinapemba, M'mwazi mwanga muli phindu lanji, potsikira ine kudzenje? Ngati fumbi lidzayamika Inu? Ngati lidzalalikira choonadi chanu? Mverani, Yehova, ndipo ndichitireni chifundo, Yehova, mundithandize ndi Inu. Munasanduliza kulira kwanga kukhale kusekera; munandivula chiguduli changa, ndipo munandiveka chikondwero, kuti ulemu wanga uimbire Inu, wosakhala chete. Yehova Mulungu wanga, ndidzakuyamikani nthawi zonse. Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide. Ndakhulupirira Inu, Yehova, ndikhale wopanda manyazi nthawi zonse, mwa chilungamo chanu ndipulumutseni ine. Munditcherere khutu lanu; ndipulumutseni msanga. Mundikhalire ine thanthwe lolimba, nyumba yamalinga yakundisunga. Pakuti Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa; ndipo chifukwa cha dzina lanu ndiyendetseni bwino, ndipo nditsogolereni. Mundionjole m'ukonde umene ananditchera mobisika. Pakuti Inu ndinu mphamvu yanga. Ndipereka mzimu wanga m'dzanja lanu; mwandiombola, Inu Yehova, Mulungu wa choonadi. Ndikwiya nao iwo akusamala zachabe zonama, koma ndikhulupirira Yehova. Ndidzakondwera ndi kusangalala m'chifundo chanu, pakuti mudapenya zunzo langa; ndipo mudadziwa mzimu wanga mu nsautso yanga. Ndipo simunandipereka m'dzanja la mdani; munapondetsa mapazi anga pali malo. Mundichitire chifundo, Yehova, pakuti ndasautsika ine. Diso langa, mzimu wanga, ndi mimba yanga, zapuwala ndi mavuto. Pakuti moyo wanga watha ndi chisoni, ndi zaka zanga zatha ndi kuusa moyo. Mphamvu yanga yafooka chifukwa cha kusakaza kwanga, ndi mafupa anga apuwala. Ndakhala chotonza chifukwa cha akundisautsa onse, inde, koposa kwa anansi anga; ndipo anzanga andiyesa choopsa; iwo akundipenya pabwalo anandithawa. Ndaiwalika m'mtima monga wakufa, ndikhala monga chotengera chosweka. Pakuti ndamva ugogodi wa ambiri, mantha andizinga. Pondipangira chiwembu, anatsimikiza mtima kulanda moyo wanga. Koma ine ndakhulupirira Inu, Yehova, ndinati, Inu ndinu Mulungu wanga. Nyengo zanga zili m'manja mwanu, mundilanditse m'manja a adani anga, ndi kwa iwo akundilondola ine. Walitsani nkhope yanu pa mtumiki wanu, mundipulumutse ndi chifundo chanu. Yehova, musandichititse manyazi; pakuti ndafuulira kwa Inu, oipa achite manyazi, atonthole m'manda. Ikhale yosalankhula milomo ya mabodza, imene imalankhula mwachipongwe pa olungama mtima, ndi kudzikuza ndi kunyoza. Ha! Kukoma kwanu ndiko kwakukulu nanga, kumene munasungira iwo akuopa Inu, kumene munachitira iwo akukhulupirira Inu, pamaso pa ana a anthu! Pobisalira pamaso panu mudzawabisa kwa chiwembu cha munthu, mudzawabisa iwo mumsasa kuti muwalanditse pa kutetana kwa malilime. Wolemekezeka Yehova, pakuti anandichitira chifundo chake chodabwitsa m'mudzi walinga. Ndipo ine, pakutenga nkhawa, ndinati, Ndadulidwa kundichotsa pamaso panu. Komatu munamva mau a kupemba kwanga pamene ndinafuulira kwa Inu. Kondani Yehova, Inu nonse okondedwa ake, Yehova asunga okhulupirika, ndipo abwezera zochuluka iye wakuchita zodzitama. Limbikani ndipo Iye adzalimbitsa mtima wanu, inu nonse akuyembekeza Yehova. Salimo la Davide. Chilangizo. Wodala munthuyo wokhululukidwa tchimo lake; wokwiriridwa choipa chake. Wodala munthuyu Yehova samwerengera mphulupulu zake; ndimo mumzimu mwake mulibe chinyengo. Pamene ndinakhala chete mafupa anga anakalamba ndi kubuula kwanga tsiku lonse. Chifukwa usana ndi usiku dzanja lanu linandilemera ine; uwisi wanga unasandulika kuuma kwa malimwe. Ndinavomera choipa changa kwa Inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibisa. Ndinati, Ndidzaululira Yehova machimo anga; ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga. Chifukwa chake oyera mtima onse apemphere kwa Inu, pa nthawi ya kupeza Inu; indetu pakusefuka madzi aakulu sadzamfikira iye. Inu ndinu mobisalira mwanga; m'nsautso mudzandisunga; mudzandizinga ndi nyimbo za chipulumutso. Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang'ana iwe. Musakhale monga kavalo, kapena ngati bulu, wopanda nzeru; zomangira zao ndizo cham'kamwa ndi chapamutu zakuwakokera, pakuti ukapanda kutero sadzakuyandikiza. Zisoni zambiri zigwera woipa; koma chifundo chidzamzinga iye wakukhulupirira Yehova. Sekerani mwa Yehova, ndimo kondwerani inu olungama mtima; ndipo fuulani mokondwera nonsenu oongoka mtima. Fuulani mokondwera mwa Yehova, inu olungama mtima, oongoka mtima ayenera kulemekeza. Yamikani Yehova ndi zeze; muimbireni ndi chisakasa cha zingwe khumi. Mumuimbire Iye nyimbo yatsopano; muimbe mwaluso kumveketsa mau. Pakuti mau a Yehova ali olunjika; ndi ntchito zake zonse zikhulupirika. Iye ndiye wakukonda chilungamo ndi chiweruzo, dziko lapansi ladzala ndi chifundo cha Yehova. Zakumwamba zinalengedwa ndi mau a Yehova; ndipo ndi mpweya wa m'kamwa mwake khamu lao lonse. Amaunjika madzi a m'nyanja monga mulu, amakundika zakuya mosungiramo. Dziko lonse lapansi liope Yehova, ponse pali anthu achite mantha chifukwa cha Iye. Pakuti ananena, ndipo chinachitidwa; analamulira, ndipo chinakhazikika. Yehova aphwanya upo wa amitundu, asandutsa chabe zolingirira za mitundu ya anthu. Chiweruzo cha Yehova chikhazikika chikhazikikire, zolingirira za m'mtima mwake ku mibadwomibadwo. Wodalitsika mtundu wa anthu umene Yehova ndiye Mulungu wao; mtundu womwe anausankha ukhale cholandira cha Iye yekha. Yehova apenyerera m'mwamba; aona ana onse a anthu. M'malo akhalamo Iye, amapenya pansi pa onse akukhala m'dziko lapansi. Iye amene akonza mitima ya iwo onse, amene azindikira zochita zao zonse. Palibe mfumu yoti gulu lalikulu limpulumutsa, mphamvu yaikulu siichilanditsa chiphona. Kavalo safikana kupulumuka naye, chinkana mphamvu yake njaikulu sapulumutsa. Taonani, diso la Yehova lili pa iwo akumuopa Iye, pa iwo akuyembekeza chifundo chake. Kupulumutsa moyo wao kwa imfa, ndi kuwasunga ndi moyo m'nyengo ya njala. Moyo wathu walindira Yehova; Iye ndiye thandizo lathu ndi chikopa chathu. Pakuti mtima wathu udzakondwera mwa Iye, chifukwa takhulupirira dzina lake loyera. Yehova, chifundo chanu chikhale pa ife, monga takuyembekezani Inu. Salimo la Davide. Muja anasintha makhalidwe ake pamaso pa Abimeleki, amene anampirikitsa, ndipo anachoka. Ndidzalemekeza Yehova nyengo zonse; kumlemekeza kwake kudzakhala m'kamwa mwanga kosalekeza. Moyo wanga udzatamanda Yehova; ofatsa adzakumva nadzakondwera. Bukitsani pamodzi ndine ukulu wa Yehova, ndipo tikweze dzina lake pamodzi. Ndinafuna Yehova ndipo anandivomera, nandilanditsa m'mantha anga onse. Iwo anayang'ana Iye nasanguluka; ndipo pankhope pao sipadzachita manyazi. Munthu uyu wozunzika anafuula, ndipo Yehova anamumva, nampulumutsa m'masautso ake onse. Mngelo wa Yehova azinga kuwatchinjiriza iwo akuopa Iye, nawalanditsa iwo. Talawani, ndipo onani kuti Yehova ndiye wabwino; wodala munthuyo wakukhulupirira Iye. Opani Yehova, inu oyera mtima ake; chifukwa iwo akumuopa Iye sasowa. Misona ya mkango isowa nimva njala, koma iwo akufuna Yehova sadzasowa kanthu kabwino. Idzani ananu ndimvereni ine, ndidzakulangizani zakumuopa Yehova. Munthu wokhumba moyo ndani, wokonda masiku, kuti aone zabwino? Uletse lilime lako lisatchule zoipa, ndipo milomo yako isalankhule chinyengo. Futuka pazoipa, nuchite zabwino, funa mtendere ndi kuulondola. Maso a Yehova ali pa olungama mtima, ndipo makutu ake atchereza kulira kwao. Nkhope ya Yehova itsutsana nao akuchita zoipa, kudula chikumbukiro chao pa dziko lapansi. Iwowo anaitana, ndipo Yehova anawamva, nawalanditsa kumasautso ao onse. Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi. Masautso a wolungama mtima achuluka, koma Yehova amlanditsa mwa onsewa. Iye asunga mafupa ake onse; silinathyoka limodzi lonse. Mphulupulu idzamupha woipa; ndipo adzawatsutsa kumlandu iwo akudana naye wolungama. Yehova aombola moyo wa anyamata ake, ndipo sadzawatsutsa kumlandu onse akukhulupirira Iye. Salimo la Davide. Tsutsanani nao iwo akutsutsana nane, Yehova; limbanani nao iwo akulimbana nane. Gwirani chikopa chotchinjiriza, ukani kundithandiza. Sololani nthungo, ndipo muwatsekerezere kunjira akundilondola. Nenani ndi moyo wanga, Chipulumutso chako ndine. Athe nzeru nachite manyazi iwo akufuna moyo wanga; abwezedwe m'mbuyo nasokonezeke iwo akundipangira chiwembu. Akhale monga mungu kumphepo, ndipo mngelo wa Yehova awapirikitse. Njira yao ikhale ya mdima ndi yoterera, ndipo mngelo wa Yehova awalondole. Pakuti ananditchera ukonde wao m'mbunamo kopanda chifukwa, anakumbira moyo wanga dzenje kopanda chifukwa. Chimgwere modzidzimutsa chionongeko; ndipo ukonde wake umene anautcha umkole yekha mwini, agwemo, naonongeke m'mwemo. Ndipo moyo wanga udzakondwera mwa Yehova; udzasekera mwa chipulumutso chake. Mafupa anga onse adzanena, Yehova, afanana ndi Inu ndani, wakulanditsa wozunzika kwa iye amene amposa mphamvu, ndi wozunzika ndi waumphawi kwa iye amfunkhira? Mboni za chiwawa ziuka, zindifunsa zosadziwa ine. Andibwezera choipa m'malo mwa chokoma, inde, asaukitsa moyo wanga. Koma ine, pakudwala iwowa, chovala changa ndi chiguduli. Ndinazunza moyo wanga ndi kusala; ndipo pemphero langa linabwera kuchifuwa changa. Ndakhala ine monga ngati iye anali bwenzi langa, kapena mbale wanga; polira ndinaweramira pansi, monga munthu wakulira maliro amai wake. Ndipo pakutsimphina ine anakondwera, nasonkhana pamodzi; akundipanda anandisonkhanira; ndipo sindinachidziwa, ananding'amba osaleka. Pakati pa onyodola pamadyerero, anandikukutira mano. Ambuye, mudzapenyererabe nthawi yanji? Bwezani moyo wanga kwa zakundiononga zao, wanga wa wokha kwa misona ya mkango. Ndidzakuyamikani mu msonkhano waukulu; m'chikhamu cha anthu ndidzakulemekezani. Adani anga asandikondwerere ine monyenga; okwiya nane kopanda chifukwa asanditsinzinire. Pakuti salankhula zamtendere, koma apangira chiwembu odekha m'dziko. Ndipo andiyasamira m'kamwa mwao; nati, Hede, Hede, diso lathu lidachipenya. Yehova, mudazipenya; musakhale chete, Ambuye, musakhale kutali ndi ine. Galamukani, ndipo khalani maso kundiweruzira mlandu wanga, Mulungu wanga ndi Ambuye wanga. Mundiweruze monga mwa chilungamo chanu, Yehova Mulungu wanga; ndipo asandisekerere ine. Asanene mumtima mwao, Hede, momwemo! Asanene, Tammeza iye. Achite manyazi, nadodome iwo akukondwera chifukwa cha choipa chidandigwera. Avekeke ndi manyazi ndi kupunzika iwo akudzikuza pa ine. Afuule mokondwera nasangalale iwo akukondwera nacho chilungamo changa, ndipo anene kosalekeza, Abuke Yehova, amene akondwera ndi mtendere wa mtumiki wake. Ndipo lilime langa lilalikire chilungamo chanu, ndi lemekezo lanu tsiku lonse. Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide, mtumiki wa Yehova. Cholakwa cha woipayo chimati m'kati mwa mtima wanga, palibe kuopa Mulungu pamaso pake. Pakuti adzidyoletsa yekha m'kuona kwake, kuti anthu sadzachipeza choipa chake ndi kukwiya nacho. Mau a pakamwa pake ndiwo opanda pake ndi onyenga, waleka kuzindikira ndi kuchita bwino. Alingirira zopanda pake pakama pake; adziika panjira posati pabwino; choipa saipidwa nacho. Yehova, m'mwamba muli chifundo chanu; choonadi chanu chifikira kuthambo. Chilungamo chanu chikunga mapiri a Mulungu; maweruzo anu akunga chozama chachikulu, Yehova, musunga munthu ndi nyama. Ha! Chifundo chanu, Mulungu, nchokondedwadi! Ndipo ana a anthu athawira kumthunzi wa mapiko anu. Adzakhuta kwambiri ndi zonona za m'nyumba mwanu, ndipo mudzawamwetsa mu mtsinje wa zokondweretsa zanu. Pakuti chitsime cha moyo chili ndi Inu, M'kuunika kwanu tidzaona kuunika. Tanimphitsani chifundo chanu pa iwo akudziwa Inu; ndi chilungamo chanu pa oongoka mtima. Phazi la akudzikuza lisandifikire ine, ndi dzanja la oipa lisandichotse. Pomwepo padagwera ochita zopanda pake. Anawalikha, ndipo sadzatha kuukanso. Salimo la Davide. Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa, usachite nsanje chifukwa cha ochita chosalungama. Pakuti adzawamweta msanga monga udzu, ndipo adzafota monga msipu wauwisi. Khulupirira Yehova, ndipo chita chokoma; khala m'dziko, ndipo tsata choonadi. Udzikondweretsenso mwa Yehova; ndipo Iye adzakupatsa zokhumba mtima wako. Pereka njira yako kwa Yehova; khulupiriranso Iye, adzachichita. Ndipo adzaonetsa chilungamo chako monga kuunika, ndi kuweruza kwako monga usana. Khala chete mwa Yehova, numlindirire Iye; usavutike mtima chifukwa cha iye wolemerera m'njira yake, chifukwa cha munthu wakuchita chiwembu. Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo; usavutike mtima ungachite choipa. Pakuti ochita zoipa adzadulidwa; koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi. Katsala kanthawi ndipo woipa adzatha psiti; inde, udzayang'anira mbuto yake, nudzapeza palibe. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nao mtendere wochuluka. Woipa apangira chiwembu wolungama, namkukutira mano. Ambuye adzamseka, popeza apenya kuti tsiku lake likudza. Oipa anasolola lupanga, nakoka uta wao; alikhe ozunzika ndi aumphawi, aphe amene ali oongoka m'njira. Lupanga lao lidzalowa m'mtima mwao momwe, ndipo mauta ao adzathyoledwa. Zochepa zake za wolungama zikoma koposa kuchuluka kwao kwa oipa ambiri. Pakuti manja a oipa adzathyoledwa, koma Yehova achirikiza olungama. Yehova adziwa masiku a anthu angwiro; ndipo chosiyira chao chidzakhala chosatha. Sadzachita manyazi m'nyengo yoipa, ndipo m'masiku a njala adzakhuta. Pakuti oipa adzatayika, ndipo adani ake a Yehova adzanga mafuta a anaankhosa; adzanyeka, monga utsi adzakanganuka. Woipa akongola, wosabweza, koma wolungama achitira chifundo, napereka. Pakuti iwo amene awadalitsa adzalandira dziko lapansi; koma iwo amene awatemberera adzadulidwa. Yehova akhazikitsa mayendedwe a munthu; ndipo akondwera nayo njira yake. Angakhale akagwa, satayikiratu, pakuti Yehova agwira dzanja lake. Ndinali mwana ndipo ndakalamba; ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya. Tsiku lonse achitira chifundo, nakongoletsa; ndipo mbumba zake zidalitsidwa. Siyana nacho choipa, nuchite chokoma, nukhale nthawi zonse. Pakuti Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa ake. Asungika kosatha, koma adzadula mbumba za oipa. Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha. Pakamwa pa wolungama palankhula zanzeru, ndi lilime lake linena chiweruzo. Malamulo a Mulungu wake ali mumtima mwake; pakuyenda pake sadzaterereka. Woipa aunguza wolungama, nafuna kumupha. Yehova sadzamsiya m'dzanja lake; ndipo sadzamtsutsa poweruzidwa iye. Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko. Pakudulidwa oipa udzapenya. Ndapenya woipa, alikuopsa, natasa monga mtengo wauwisi wanzika. Koma anapita ndipo taona, kwati zii; ndipo ndinampwaira osampeza. Tapenya wangwiro, ndipo taona woongoka mtima! Pakuti ku matsiriziro ake a munthuyo kuli mtendere. Koma olakwa adzaonongeka pamodzi; matsiriziro a oipa adzadulidwa. Koma chipulumutso cha olungama chidzera kwa Yehova, Iye ndiye mphamvu yao m'nyengo ya nsautso. Ndipo Yehova awathandiza, nawalanditsa; awalanditsa kwa oipa nawapulumutsa, chifukwa kuti anamkhulupirira Iye. Salimo la Davide, lakukumbutsa. Yehova, musandidzudzule ndi mkwiyo wanu, ndipo musandilange moopsa m'mtima mwanu. Pakuti mivi yanu yandilowa, ndi dzanja lanu landigwera. Mumnofu mwanga mulibe chamoyo chifukwa cha ukali wanu; ndipo m'mafupa anga simuzizira, chifukwa cha cholakwa changa. Pakuti mphulupulu zanga zapitirira pamutu panga; ndathodwa nazo monga ndi katundu wolemera. Mabala anga anunkha, adaola, chifukwa cha kupusa kwanga. Ndapindika, ndawerama kwakukulu; ndimayenda woliralira tsiku lonse. Pakuti m'chuuno mwanga mutentha kwambiri; palibe pamoyo m'mnofu mwanga. Ndafooka ine, ndipo ndachinjizidwa, ndabangula chifukwa cha kumyuka mtima wanga. Ambuye, chikhumbo changa chonse chili pamaso panu; ndipo kubuula kwanga sikubisika kwa Inu. Mtima wanga ugundagunda, mphamvu yanga yachoka, ndipo kuunika kwa maso anga, ndi iko komwe kwandichokera. Ondikonda ndi anzanga apewa mliri wanga; ndipo anansi anga aima patali. Ndipo anditchera misampha iwo akufuna moyo wanga; ndipo iwo akuyesa kundichitira choipa alankhula zoononga, nalingirira zonyenga tsiku lonse. Koma ine, monga gonthi, sindimva; ndipo monga munthu wosalankhula, sinditsegula pakamwa panga. Inde ndikunga munthu wosamva, ndipo m'kamwa mwanga mulibe makani. Pakuti ndikuyembekezani Inu, Yehova; Inu mudzayankha, Ambuye Mulungu wanga. Pakuti ndinati, Asakondwerere ine; pakuterereka phazi langa, asadzikuze pa ine. Ndafikana potsimphina, ndipo chisoni changa chili pamaso panga chikhalire. Pakuti ndidzafotokozera mphulupulu yanga; nditenga nkhawa chifukwa cha tchimo langa. Koma adani anga ali ndi moyo, nakhala ndi mphamvu, ndipo akundida kopanda chifukwa achuluka. Ndipo iwo akubwezera choipa pa chabwino atsutsana nane, popeza nditsata chabwino. Musanditaye, Yehova, Mulungu wanga, musakhale kutali ndi ine. Fulumirani kundithandiza, Ambuye, chipulumutso changa. Kwa Mkulu wa Nyimbo, kwa Yedutuni. Salimo la Davide. Ndinati, Ndidzasunga njira zanga, kuti ndingachimwe ndi lilime langa. Ndidzasunga pakamwa panga ndi cham'kamwa, pokhala woipa ali pamaso panga. Ndinatonthola osanena mau, ndinakhala chete osalawa chokoma; ndipo chisoni changa chinabuka. Mtima wanga unatentha m'kati mwa ine; unayaka moto pakulingirira ine. Pamenepo ndinalankhula ndi lilime langa, Yehova, mundidziwitse chimaliziro changa, ndi mawerengedwe a masiku anga ndi angati; ndidziwe malekezero anga. Onani, munaika masiku anga akhale monga kuyesa dzanja; ndipo zaka zanga zili ngati chabe pamaso panu, Indedi munthu aliyense angakhale wokhazikika, ali chabe konse. Indedi munthu ayenda ngati mthunzi; Indedi avutika chabe: Asonkhanitsa chuma, ndipo sadziwa adzachilandira ndani? Ndipo tsopano, Ambuye, ndilindira chiyani? Chiyembekezo changa chili pa Inu. Ndipulumutseni kwa zolakwa zanga zonse, musandiike ndikhale chotonza cha wopusa. Ndinakhala duu, sindinatsegula pakamwa panga; chifukwa inu mudachichita. Mundichotsere chovutitsa chanu; pandithera ine chifukwa cha kulanga kwa dzanja lanu. Pamene mulanga munthu ndi zomdzudzula chifukwa cha mphulupulu, mukanganula kukongola kwake monga mumachita ndi njenjete. Indedi, munthu aliyense ali chabe. Imvani pemphero langa, Yehova, ndipo tcherani khutu kulira kwanga; musakhale chete pa misozi yanga; Pakuti ine ndine mlendo ndi Inu, wosakhazikika, monga makolo anga onse. Ndiloleni, kuti nditsitsimuke, ndisanamuke ndi kukhala kuli zii. Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide. Kuyembekeza ndayembekeza Yehova; ndipo anandilola, namva kufuula kwanga. Ndipo anandikweza kunditulutsa m'dzenje la chitayiko, ndi m'thope la pachithaphwi; nandipondetsa pathanthwe, nakhazika mayendedwe anga. Ndipo anapatsa nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, chilemekezo cha kwa Mulungu wanga; ambiri adzachiona, nadzaopa, ndipo adzakhulupirira Yehova. Wodala munthuyo wakuyesa Yehova wokhulupirika; wosasamala odzikuza, ndi opatukira kubodza. Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwitsa zanu mudazichita nzambiri, ndipo zolingirira zanu za pa ife; palibe wina wozifotokozera Inu; ndikazisimba ndi kuzitchula, zindichulukira kuziwerenga. Nsembe ndi chopereka simukondwera nazo; mwanditsegula makutu. Nsembe yopsereza ndi yamachimo simunapempha. Pamenepo ndinati, Taonani, ndadza; m'buku mwalembedwa za Ine, kuchita chikondwero chanu kundikonda, Mulungu wanga; ndipo malamulo anu ali m'kati mwamtima mwanga. Ndalalikira chilungamo mu msonkhano waukulu; onani, sindidzaletsa milomo yanga, mudziwa ndinu Yehova. Chilungamo chanu sindinachibisa m'kati mwamtima mwanga; chikhulupiriko chanu ndi chipulumutso chanu ndinachinena; chifundo chanu ndi choonadi chanu sindinachibisira msonkhano waukulu. Inu Yehova, simudzandikaniza nsoni zanu, chifundo chanu ndi choonadi chanu zindisunge chisungire. Pakuti zoipa zosawerengeka zandizinga, zochimwa zanga zandipeza kotero kuti sindikhoza kupenya; ziposa tsitsi la mutu wanga, ndipo wandichokera mtima. Ndikupemphani, Yehova, ndilanditseni; fulumirani kudzandithandiza, Yehova. Achite manyazi nadodome iwo akulondola moyo wanga kuti auononge. Abwerere m'mbuyo, nachite manyazi iwo okondwera kundichitira choipa. Apululuke, mobwezera manyazi ao amene anena nane, Hede, hede. Asekerere nakondwerere mwa Inu onse akufuna Inu; iwo akukonda chipulumutso chanu asaleke kunena, Abuke Yehova. Ndipo ine ndine wozunzika ndi waumphawi; koma Ambuye andikumbukira ine. Inu ndinu mthandizi wanga, ndi Mpulumutsi wanga, musamachedwa, Mulungu wanga. Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide. Wodala iye amene asamalira wosauka! Tsiku la tsoka Yehova adzampulumutsa. Yehova adzamsunga, nadzamsunga ndi moyo, ndipo adzadalitsika pa dziko lapansi, ndipo musampereke ku chifuniro cha adani ake. Yehova adzamgwiriziza pa kama wodwalira; podwala iye mukonza pogona pake. Ndinati ine, Mundichitire chifundo, Yehova; Chiritsani mtima wanga; pakuti ndachimwira Inu. Adani anga andinenera choipa, ndi kuti, adzafa liti, ndi kutayika dzina lake? Ndipo akadza kundiona wina angonena bodza; mumtima mwake adzisonkhera zopanda pake, akanka nayenda namakanena. Onse akudana nane andinong'onezerana; apangana chondiipsa ine. Chamgwera chinthu choopsa, ati; popeza ali gonire sadzaukanso. Ngakhale bwenzi langa lenileni, amene ndamkhulupirira, ndiye amene adadyako mkate wanga, anandikwezera chidendene chake. Koma Inu, Yehova, mundichitire chifundo, ndipo mundiutse, kuti ndiwabwezere. Umo ndidziwa kuti mukondwera ndi ine, popeza mdani wanga sandiseka. Ndipo ine, mundigwirizize m'ungwiro wanga, ndipo mundiike pankhope panu kunthawi yamuyaya. Wodalitsika Yehova, Mulungu wa Israele, kuchokera nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha. Amen, ndi Amen. Kwa Mkulu wa Nyimbo. Chilangizo cha kwa ana a Kora. Monga nswala ipuma wefuwefu kukhumba mitsinje; motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba Inu, Mulungu. Moyo wanga uli ndi ludzu la kwa Mulungu, la kwa Mulungu wamoyo. Ndikadze liti kuoneka pamaso pa Mulungu? Misozi yanga yakhala ngati chakudya changa, usana ndi usiku; pakunena iwo kwa ine dzuwa lonse, Mulungu wako ali kuti? Ndidzikumbukira izi ndipo nditsanulira moyo wanga m'kati mwa ine, pakuti ndidafopita ndi unyinji wa anthu, ndinawatsogolera kunyumba ya Mulungu, ndi mau akuimbitsa ndi kuyamika, ndi unyinji wakusunga dzuwa lokondwera. Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu, pakuti ndidzamyamikanso chifukwa cha chipulumutso cha nkhope yake. Mulungu wanga, moyo wanga udziweramira m'kati mwanga; chifukwa chake ndikumbukira Inu m'dziko la Yordani, ndi mu Aheremoni, m'kaphiri ka Mizara. Madzi akuya aitanizana ndi madzi akuya, pa mkokomo wa matiti anu; mafunde onse a nyondonyondo anandimiza ine. Koma usana Yehova adzalamulira chifundo chake, ndipo usiku nyimbo yake idzakhala ndi ine. Inde pemphero la kwa Yehova wa moyo wanga. Ndidzati kwa Mulungu, thanthwe langa, mwandiiwala chifukwa ninji? Ndimayenderanji wakulira chifukwa cha kundipsinja mdaniyo? Adani anga andinyoza ndi kundithyola mafupa anga; pakunena ndine dzuwa lonse, Mulungu wako ali kuti? Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu; pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga. Mundiweruzire, Mulungu, ndipo mundinenere mlandu kwa anthu opanda chifundo. Mundilanditse kwa munthu wonyenga ndi wosalungama. Pakuti Inu ndinu Mulungu wa mphamvu yanga; mwanditayiranji? Ndimayenderanji woliralira chifukwa cha kundipsinja mdani? Tumizirani kuunika kwanu ndi choonadi chanu zinditsogolere; zindifikitse kuphiri lanu loyera, kumene mukhala Inuko. Kuti ndipite kufikira guwa la nsembe la Mulungu, kufikira Mulungu wa chimwemwe changa chenicheni, ndi kuti ndikuyamikeni ndi zeze, Mulungu, Mulungu wanga. Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu: pakuti ndidzamyamikanso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga, ndi Mulungu wanga. Kwa Mkulu wa Nyimbo. Chilangizo cha kwa ana a Kora. Mulungu, tidamva m'makutu mwathu, makolo athu anatisimbira, za ntchitoyo mudaichita masiku ao, masiku akale. Inu munapirikitsa amitundu ndi dzanja lanu, koma iwowa munawaoka; munasautsa mitundu ya anthu, ndipo munawaingitsa. Pakuti sanalande dziko ndi lupanga lao, ndipo mkono wao sunawapulumutse. Koma dzanja lanu lamanja, ndi mkono wanu, ndi kuunika kwa nkhope yanu. Popeza munakondwera nao, Inu ndinu mfumu yanga, Mulungu; lamulirani chipulumutso cha Yakobo. Mwa Inu tidzakankhira pansi otsutsana nafe, m'dzina lanu tidzapondereza akutiukira ife. Pakuti sinditama uta wanga, ndipo lupanga langa silingandipulumutse. Koma Inu munatipulumutsa kwa iwo akutsutsana nafe, ndipo akudana nafe, mudawachititsa manyazi. Mwa Mulungu tidzitamanda tsiku lonse, ndipo dzina lanu tidzaliyamika kosatha. Koma mwatitaya, ndi kutinyazitsa; ndipo simutuluka nao makamu a nkhondo athu. Mutibwereretsa kuthawa otisautsa, ndipo akudana nafe adzifunkhira okha. Mwatipereka ngati nkhosa zoyenera kuzidya; ndipo mwatibalalitsa mwa amitundu. Mugulitsa anthu anu kwachabe, ndipo mtengo wake simupindula nao. Mutisandutsa chotonza kwa anzathu, ndi choseketsa ndi cholalatitsa iwo akutizinga. Mutiika tikhale onyozeka mwa amitundu, ndi kuti anthu atipukusire mitu. Tsiku lonse chimpepulo changa chikhala pamaso panga, ndipo manyazi a pankhope panga andikuta. Chifukwa cha mau a wotonza wochitira mwano; chifukwa cha mdani ndi wobwezera chilango. Zonsezi zatigwera; koma sitinakuiwalani, ndipo sitinachita monyenga m'pangano lanu. Mtima wathu sunabwerera m'mbuyo, ndipo m'mayendedwe athu sitinapatuka m'njira yanu; mungakhale munatithyola mokhala zilombo, ndi kutiphimba nao mthunzi wa imfa. Tikadaiwala dzina la Mulungu wathu, ndi kutambasulira manja athu kwa mulungu wachilendo; Mulungu sakadasanthula ichi kodi? Pakuti adziwa zinsinsi za mtima. Koma, chifukwa cha Inu, tiphedwa tsiku lonse; tiyesedwa ngati nkhosa zakuzipha. Galamukani, mugoneranji, Ambuye? Ukani, musatitaye chitayire. Mubisiranji nkhope yanu, ndi kuiwala kuzunzika ndi kupsinjika kwathu? Pakuti moyo wathu waweramira kufumbi, pamimba pathu pakangamira dziko lapansi. Ukani, tithandizeni, tiomboleni mwa chifundo chanu. Kwa Mkulu wa Nyimbo, pa Syosyanimu. Chilangizo cha kwa ana a Kora. Nyimbo ya chikondi. Mtima wanga usefukira nacho chinthu chokoma. Ndinena zopeka ine za mfumu, lilime langa ndilo peni yofulumiza kulemba. Inu ndinu wokongola ndithu koposa ana a anthu; anakutsanulirani chisomo pa milomo yanu, chifukwa chake Mulungu anakudalitsani kosatha. Dzimangireni lupanga lanu m'chuuno mwanu, wamphamvu inu, ndi ulemerero wanu ndi ukulu wanu. Ndipo pindulani, m'ukulu wanu yendani, kaamba ka choonadi ndi chifatso ndi chilungamo; ndipo dzanja lanu lidzakuphunzitsani zoopsa. Mivi yanu njakuthwa; mitundu ya anthu igwa pansi pa inu; iwalasa mumtima adani a mfumu. Mpando wachifumu wanu, Mulungu, ukhala nthawi zonse zomka muyaya. Ndodo yachifumu ya ufumu wanu ndiyo ndodo yolunjika. Mukonda chilungamo, ndipo mudana nacho choipa, chifukwa chake Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wadzoza inu ndi mafuta a chikondwerero koposa anzanu. Zovala zanu zonse nza mure, ndi khonje, ndi kasiya; m'zinyumba za mfumu zomanga ndi minyanga ya njovu mwatuluka zoimba za zingwe zokukondweretsani. Mwa omveka anu muli ana akazi a mafumu; ku dzanja lanu lamanja aima mkazi wa mfumu wovala golide wa ku Ofiri. Tamvera, mwana wamkaziwe, taona, tatchera khutu lako; uiwalenso mtundu wako ndi nyumba ya atate wako; potero mfumuyo adzakhumba kukoma kwako, pakuti ndiye mbuye wako; ndipo iwe umgwadire iye. Ndipo mwana wamkazi wa Tiro adzafika nayo mphatso; achuma a mwa anthu adzapempha kudziwika nanu. Mwana wamkazi wa mfumu ngwa ulemerero wonse m'kati mwa nyumba, zovala zake nza malukidwe agolide. Adzamtsogolera kwa mfumu wovala zamawangamawanga, anamwali anzake omtsata adzafika nao kwa inu. Adzawatsogolera ndi chimwemwe ndi kusekerera, adzalowa m'nyumba ya mfumu. M'malo mwa makolo ako mudzakhala ana ako, udzawaika akhale mafumu m'dziko lonse lapansi. Ndidzawakumbutsa dzina lanu m'mibadwomibadwo; chifukwa chake mitundu ya anthu idzayamika Inu kunthawi za nthawi. Kwa Mkulu wa Nyimbo; Chilangizo cha kwa ana a Kora. Pa Alamot. Nyimbo. Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m'masautso. Chifukwa chake sitidzachita mantha, lingakhale lisandulika dziko lapansi, angakhale mapiri asunthika, nakhala m'kati mwa nyanja. Chinkana madzi ake akokoma, nachita thovu, nagwedezeka mapiri ndi kudzala kwake. Pali mtsinje, ngalande zake zidzakondweretsa mudzi wa Mulungu. Malo oyera okhalamo Wam'mwambamwamba. Mulungu ali m'kati mwake, sudzasunthika, Mulungu adzauthandiza mbandakucha. Amitundu anapokosera, maufumu anagwedezeka, ananena mau, dziko lapansi linasungunuka. Yehova wa makamu ali ndi ife; Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu. Idzani, penyani ntchito za Yehova, amene achita zopululutsa pa dziko lapansi. Aletsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi; athyola uta, nadula nthungo; atentha magaleta ndi moto. Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka pa dziko lapansi. Yehova wa makamu ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu. Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la ana a Kora. Ombani m'manja, mitundu yonse ya anthu; fuulirani kwa Mulungu ndi liu la kuimbitsa. Pakuti Yehova Wam'mwambamwamba ndiye woopsa; ndiye mfumu yaikulu pa dziko lonse lapansi. Atigonjetsera anthu, naika amitundu pansi pa mapazi athu. Atisankhira cholowa chathu, chokometsetsa cha Yakobo amene anamkonda. Mulungu wakwera ndi mfuu, Yehova ndi liu la lipenga. Imbirani Mulungu, imbirani; imbirani mfumu yathu, imbirani. Pakuti Mulungu ndiye mfumu ya dziko lonse lapansi; imbirani ndi chilangizo. Mulungu ndiye mfumu ya amitundu, Mulungu akhala pa mpando wachifumu wake woyera. Akulu a anthu asonkhana akhale anthu a Mulungu wa Abrahamu, pakuti zikopa za dziko lapansi nza Mulungu; akwezeka kwakukulu Iyeyo. Nyimbo; Salimo la ana a Kora. Yehova ndiye wamkulu, ayenera kulemekezekadi, m'mudzi wa Mulungu wathu, m'phiri lake loyera. Phiri la Ziyoni, chikhalidwe chake nchokoma kumbali zake za kumpoto, ndilo chimwemwe cha dziko lonse lapansi, mudzi wa mfumu yaikulu. Mulungu adziwika m'zinyumba zake ngati msanje. Pakuti, taonani, mafumuwo anasonkhana, anapitira pamodzi. Anapenya mudziwo, ndipo pamenepo anadabwa; anaopsedwa, nathawako. Pomwepo anagwidwa nako kunthunthumira; anamva chowawa, ngati wam'chikuta. Muswa zombo za ku Tarisisi ndi mphepo ya kum'mawa. Monga tidamva, momwemo tidapenya m'mudzi wa Yehova wa makamu, m'mudzi wa Mulungu wathu, Mulungu adzaukhazikitsa kunthawi yamuyaya. Tidalingalira zachifundo chanu, Mulungu, m'kati mwa Kachisi wanu. Monga dzina lanu, Mulungu, momwemo lemekezo lanu ku malekezero a dziko lapansi; m'dzanja lamanja lanu mudzala chilungamo. Likondwere phiri la Ziyoni, asekere ana akazi a Yuda, chifukwa cha maweruzo anu. Zungulirani Ziyoni, ndipo muuzinge, werengani nsanja zake. Penyetsetsani malinga ake, yesetsani zinyumba zake; kuti mukaziwerengere mibadwo ikudza m'mbuyo. Pakuti Mulungu ameneyo ndiye Mulungu wathu kunthawi za nthawi, adzatitsogolera kufikira imfa. Kwa Mkulu wa Nyimbo; Salimo la ana a Kora. Dzamveni kuno, anthu inu nonse; tcherani khutu, inu nonse amakono, awamba ndi omveka omwe, achuma ndi aumphawi omwe. Pakamwa panga padzanena zanzeru; ndipo chilingiriro cha mtima wanga chidzakhala cha chidziwitso. Ndidzatchera khutu kufanizo, ndidzafotokozera chophiphiritsa changa poimbira. Ndidzaoperanji masiku oipa, pondizinga amphulupulu onditsata kuchidendene? Iwo akutama kulemera kwao; nadzitamandira pa kuchuluka kwa chuma chao; kuombola mbale sangadzamuombole, kapena kumperekera dipo kwa Mulungu. Popeza chiombolo cha moyo wao ncha mtengo wake wapatali, ndipo chilekeke nthawi zonse. Kuti akhale ndi moyo osafa, osaona chivundi. Pakuti aona anzeru amafa, monga aonongekera wopusa, wodyerera momwemo, nasiyira ena chuma chao. Mumtima mwao ayesa kuti nyumba zao zikhala chikhalire, ndi mokhala iwo ku mibadwomibadwo; atchapo dzina lao padziko pao. Koma munthu wa ulemu wake sakhalitsa, afanana ndi nyama za kuthengo, afanana nazo. Njira yao yino ndiyo kupusa kwao, koma akudza m'mbuyo avomereza mau ao. Aikidwa m'manda ngati nkhosa; mbusa wao ndi imfa. Ndipo m'mawa mwake oongoka mtima adzakhala mafumu ao; ndipo maonekedwe ao adzanyekera kumanda, kuti pokhala pake padzasowa. Koma Mulungu adzaombola moyo wanga kumphamvu ya manda. Pakuti adzandilandira ine. Usaope polemezedwa munthu, pochuluka ulemu wa nyumba yake; pakuti pomwalira iye sadzamuka nako kanthu kalikonse; ulemu wake sutsika naye kumtsata m'mbuyo. Angakhale anadalitsa moyo wake pokhala ndi moyo, ndipo anthu akulemekeza iwe, podzichitira wekha zokoma. Adzamuka kumbadwo wa makolo ake; sadzaona kuunika nthawi zonse. Munthu waulemu, koma wosadziwitsa, afanana ndi nyama za kuthengo, afanana nazo. Salimo la Asafu. Mulungu wa milungu, Yehova, wanena, aitana dziko lapansi kuyambira kutuluka kwa dzuwa kufikira kulowa kwake. Mulungu awalira m'Ziyoni, mokongola mwangwiro. Adzafika Mulungu wathu, ndipo sadzakhala chete. Moto udzanyeka pankhope pake, ndipo pozungulira pake padzasokosera kwakukulu. Kumwamba adzaitana zakumwamba, ndi dziko lapansi, kuti aweruze anthu ake. Mundisonkhanitsire okondedwa anga; amene anapangana ndi Ine ndi nsembe. Ndipo zakumwamba zionetsera chilungamo chake; pakuti Mulungu mwini wake ndiye woweruza. Imvani, anthu anga, ndipo ndidzanena; Israele, ndipo ndidzachita mboni pa iwe, Ine Mulungu, ndine Mulungu wako. Sindikudzudzula iwe chifukwa cha nsembe zako; popeza nsembe zako zopsereza zili pamaso panga chikhalire. Sindidzatenga ng'ombe m'nyumba mwako, kapena mbuzi m'makola mwako. Pakuti zamoyo zonse za kuthengo ndi zanga, ndi ng'ombe za pa mapiri zikwi. Ndidziwa mbalame zonse za m'mapiri, ndipo nyama za kuthengo zili ndi Ine. Ndikamva njala, sindidzakuuza, pakuti dziko lonse ndi langa, ndi kudzala kwake komwe. Kodi ndidzadya nyama ya ng'ombe, kapena kumwa mwazi wa mbuzi? Pereka kwa Mulungu nsembe yachiyamiko; numchitire Wam'mwambamwamba chowinda chako. Ndipo undiitane tsiku la chisautso, ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza. Koma kwa woipa Mulungu anena, Uli nao chiyani malemba anga kulalikira, ndi kutchula pangano langa pakamwa pako? Popeza udana nacho chilangizo, nufulatira mau anga. Pakuona mbala, uvomerezana nayo, nuchita nao achigololo. Pakamwa pako mpochita zochimwa, ndipo lilime lako likonza chinyengo. Ukhala, nuneneza mbale wako; usinjirira mwana wa mai wako. Izi unazichita iwe, ndipo ndinakhala chete Ine; unayesa kuti ndifanana nawe, ndidzakudzudzula, ndi kuchilongosola pamaso pako. Dziwitsani ichi inu oiwala Mulungu, kuti ndingakumwetuleni, ndipo mungasowepo mpulumutsi. Wopereka nsembe yachiyamiko andilemekeza Ine; ndipo kwa iye wosunga mayendedwe ake ndidzamuonetsa chipulumutso cha Mulungu. Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide; m'mene anamdzera Natani mneneriyo atalowa iye kwa Bateseba. Mundichitire ine chifundo, Mulungu, monga mwa kukoma mtima kwanu; monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu mufafanize machimo anga. Mubwereze kunditsuka mphulupulu yanga, ndipo mundiyeretse kundichotsera choipa changa. Chifukwa ndazindikira machimo anga; ndipo choipa changa chili pamaso panga chikhalire. Pa Inu, Inu nokha, ndinachimwa, ndipo ndinachichita choipacho pamaso panu; kuti mukhale wolungama pakulankhula Inu, mukhalenso woyera pa kuweruza kwanu. Onani, ndinabadwa m'mphulupulu, ndipo mai wanga anandilandira m'zoipa. Onani, Inu mukondwera ndi zoonadi m'malo a m'katimo; ndipo m'malo a m'tseri mudzandidziwitsa nzeru. Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera; munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbu woposa matalala. Mundimvetse chimwemwe ndi kusekera, kuti mafupawo munawathyola akondwere. Muzibisire nkhope yanu zolakwa zanga, ndipo mufafanize mphulupulu zanga zonse. Mundilengere mtima woyera, Mulungu; mukonze mzimu wokhazikika m'kati mwanga. Musanditaye kundichotsa pamaso panu; musandichotsere Mzimu wanu Woyera. Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu; ndipo mzimu wakulola undigwirizize. Pomwepo ndidzalangiza ochimwa njira zanu; ndipo olakwa adzabwera kwa Inu. Mundilanditse kumlandu wa mwazi, Mulungu, ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; lilime langa lidzakweza nyimbo ya chilungamo chanu. Ambuye, tsegulani pa milomo yanga; ndipo pakamwa panga padzalalikira ulemekezo wanu. Pakuti simukondwera ndi nsembe, mwenzi nditapereka; nsembe yopsereza simuikonda. Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka; Inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa. Chitirani Ziyoni chokoma monga mwa kukondwera kwanu; mumange malinga a miyala a Yerusalemu. Pamenepo mudzakondwera nazo nsembe zachilungamo, ndi nsembe yopsereza ndi yopsereza yathunthu; pamenepo adzapereka ng'ombe pa guwa lanu la nsembe. Kwa Mkulu wa Nyimbo; Chilangizo cha Davide. Muja analowa Doegi Mwedomu nauza Saulo nati kwa iye, Davide walowa m'nyumba ya Ahimeleki. Udzitamandiranji ndi choipa, chiphona iwe? Chifundo cha Mulungu chikhala tsiku lonse. Lilime lako likupanga zoipa; likunga lumo lakuthwa, lakuchita monyenga. Ukonda choipa koposa chokoma; ndi bodza koposa kunena chilungamo, ukonda mau onse akuononga, lilime lachinyengo, iwe. Potero Mulungu adzakupasula kunthawi zonse, adzakuchotsa nadzakukwatula m'hema mwako, nadzakuzula, kukuchotsa m'dziko la amoyo. Ndipo olungama adzachiona, nadzaopa, nadzamseka, ndi kuti, Tapenyani, suyu munthuyu amene sanamuyese Mulungu mphamvu yake; amene anatama kuchuluka kwa chuma chake, nadzilimbitsa m'kuipsa kwake. Koma ine ndine ngati mtengo wauwisi wa azitona m'nyumba ya Mulungu. Ndikhulupirira chifundo cha Mulungu kunthawi za nthawi. Ndidzakuyamikani kosatha, popeza Inu munachichita ichi, ndipo ndidzayembekeza dzina lanu, pakuti ichi nchokoma, pamaso pa okondedwa anu. Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Mahalati. Chilangizo cha Davide. Chitsiru chimati mumtima mwake, Kulibe Mulungu. Achita zovunda, achita chosalungama chonyansa; kulibe wakuchita bwino. Mulungu m'mwamba anaweramira pa ana a anthu, kuti aone ngati aliko wanzeru, wakufuna Mulungu. Onse anabwerera; anavunda mtima pamodzi; palibe mmodzi wakuchita bwino, nnena mmodzi. Kodi ochita zopanda pake sadziwa? Pomadya anthu anga monga akudya mkate; ndipo saitana Mulungu. Pamenepo anaopa kwakukulu, popanda chifukwa cha kuopa, pakuti Mulungu anamwaza mafupa a iwo akuzinga iwe; unawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawakaniza. Ha, chipulumutso cha Israele chichokere m'Ziyoni! Pakubweretsa Mulungu anthu ake a m'ndende, Yakobo adzakondwera, Israele adzasekera. Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Neginoto. Chilangizo cha Davide. Muja Azifi anamuka nauza Saulo, kuti, Kodi Davide sabisala kwathu nanga? Ndipulumutseni, Mulungu, mwa dzina lanu, ndipo mundiweruze ndi mphamvu yanu. Imvani pemphero langa, Mulungu; tcherani khutu mau a pakamwa panga. Pakuti alendo andiukira, ndipo oopsa afunafuna moyo wanga; sadziikira Mulungu pamaso pao. Taonani, Mulungu ndiye mthandizi wanga, Ambuye ndiye wachirikiza moyo wanga. Adzabwezera choipa adani anga, aduleni m'choonadi chanu. Ine mwini ndidzapereka nsembe yaufulu kwa Inu, ndidzayamika dzina lanu, Yehova, pakuti nlokoma. Pakuti anandilanditsa m'nsautso yonse; ndipo ndapenya ndi diso langa icho ndakhumbira pa adani anga. Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Zirumbu. Chilangizo cha Davide. Tcherani khutu pemphero langa, Mulungu; ndipo musadzibisa pa kupemba kwanga. Mverani, ndipo mundiyankhe, ndiliralira m'kudandaula kwanga ndi kubuula; chifukwa cha mau a mdani, chifukwa cha kundipsinja woipa; pakuti andisenza zopanda pake, ndipo adana nane mumkwiyo. Mtima wanga uwawa m'kati mwanga; ndipo zoopsa za imfa zandigwera. Mantha ndi kunjenjemera zandidzera, ndipo zoopsetsa zandikuta. Ndipo ndinati, Ha, wina akadandipatsa mapiko onga a njiwa! Mwenzi nditauluka, ndi kukhaliratu. Onani, ndikadathawira kutali, ndikadagona m'chipululu. Ndikadafulumira ndipulumuke kumphepo yolimba ndi namondwe. Aonongeni, Ambuye, gawani lilime lao, pakuti ndaona chiwawa ndi ndeu m'mudzimo. Izizo ziuzungulira pa malinga ake usana ndi usiku; ndipo m'kati mwake muli zopanda pake ndi chovuta. M'kati mwake muli kusakaza, chiwawa ndi chinyengo sizichoka m'makwalala ake. Pakuti si mdani amene ananditonzayo; pakadatero ndikadachilola, amene anadzikuza pa ine sindiye munthu wondida; pakadatero ndikadambisalira: Koma ameneyo ndiwe, munthu woyenerana nane, tsamwali wanga, wodziwana nane. Tinapangirana upo wokoma, tinaperekeza khamu la anthu popita kunyumba ya Mulungu. Imfa iwagwere modzidzimutsa, atsikire kumanda ali amoyo, pakuti m'mokhala mwao muli zoipa pakati pao. Koma ine ndidzafuulira kwa Mulungu; ndipo Yehova adzandipulumutsa. Madzulo, m'mawa, ndi msana ndidzadandaula, ndi kubuula, ndipo adzamva mau anga. Anaombola moyo wanga kunkhondo yondilaka, ndikhale mumtendere, pakuti ndiwo ambiri okangana nane. Mulungu adzamva, nadzawasautsa, ndiye wokhalabe chiyambire kale lomwe. Popeza iwowa sasinthika konse, ndipo saopa Mulungu. Anatulutsa manja ake awagwire iwo akuyanjana naye, anaipsa pangano lake. Pakamwa pake mposalala ngati mafuta amkaka, koma mumtima mwake munali nkhondo, mau ake ngofewa ngati mafuta oyenga, koma anali malupanga osololasolola. Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza, nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke. Koma Inu, Mulungu, mudzawatsitsira kudzenje la chionongeko. Anthu okhetsa mwazi ndi achinyengo masiku ao sadzafikira nusu; koma ine ndidzakhulupirira Inu. Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Yonat-Elem-Rekokimu. Mikitamu wa Davide, muja Afilisti anamgwira m'Gati. Mundichitire chifundo, Mulungu, pakuti anthu afuna kundimeza. Andipsinja pondithira nkhondo tsiku lonse. Adani anga afuna kundimeza tsiku lonse, pakuti ambiri andithira nkhondo modzikuza. Tsiku lakuopa ine, ndidzakhulupirira Inu. Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ake, ndakhulupirira Mulungu, sindidzaopa; anthu adzandichitanji? Tsiku lonse atenderuza mau anga, zolingirira zao zonse zili pa ine kundichitira choipa. Amemezana, alalira, atchereza mapazi anga, popeza alindira moyo wanga. Kodi adzapulumuka ndi zopanda pake? Gwetsani anthu mumkwiyo, Mulungu. Muwerenga kuthawathawa kwanga, sungani misozi yanga m'nsupa yanu; kodi siikhala m'buku mwanu? Pamenepo adani anga adzabwerera m'mbuyo tsiku lakuitana ine. Ichi ndidziwa, kuti Mulungu avomerezana nane. Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ake, mwa Yehova ndidzalemekeza mau ake. Pa Mulungu ndakhulupirira, sindidzaopa; munthu adzandichitanji? Zowindira Inu Mulungu, zili pa ine, ndidzakuchitirani zoyamika. Pakuti mwalanditsa moyo wanga kuimfa, simunatero nao mapazi anga kuti ndingagwe? Kuti ndiyende pamaso pa Mulungu m'kuunika kwa amoyo. Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Altasheti; Mikitamu wa Davide: muja anathawa Saulo, ali m'phanga. Mundichitire chifundo, Mulungu, mundichitire chifundo; pakuti moyo wanga ukhulupirira Inu, ndipo ndithawira kumthunzi wa mapiko anu, kufikira zosakazazo zidzapita. Ndidzafuulira kwa Mulungu Wam'mwambamwamba; ndiye Mulungu wonditsirizira zonse. Adzanditumizira m'mwamba, nadzandipulumutsa ponditonza wofuna kundimeza; Mulungu adzatumiza chifundo chake ndi choonadi chake. Moyo wanga uli pakati pa mikango; ndigona pakati pa oyaka moto, ndiwo ana a anthu amene mano ao ali nthungo ndi mivi, ndipo lilime lao ndilo lupanga lakuthawa. Mukwezeke m'mwambamwamba, Mulungu; ulemerero wanu ukhale pamwamba pa dziko lonse lapansi. Ananditchera ukonde apo ndiyenda; moyo wanga wawerama. Anandikumbira mbuna patsogolo panga; anagwa m'kati mwake iwo okha. Mtima wanga wakhazikika, Mulungu, ndakhazika mtima; ndidzaimba, inde, ndidzaimba zolemekeza. Galamuka, ulemu wanga; galamukani chisakasa ndi zeze! Ndidzauka ndekha mamawa. Ndidzakuyamikirani mwa anthu, Ambuye, ndidzakuimbirani mwa mitundu. Pakuti chifundo chanu nchachikulu kufikira m'mwamba, ndi choonadi chanu kufikira mitambo. Kwezekani m'mwambamwamba, Mulungu; ulemerero wanu ukhale pamwamba m'dziko lonse lapansi. Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Altasyeti; Mikitamu wa Davide. Kodi muli chete ndithu poyenera inu kunena zolungama? Muweruza ana anthu molunjika kodi? Inde, mumtima muchita zosalungama; pa dziko lapansi mugawira anthu chiwawa cha m'manja mwanu. Oipa achita chilendo chibadwire, asokera kuyambira kubadwa kwao, nanena bodza. Ululu wao ukunga wa njoka; akunga mphiri yogontha m'khutu, itseka m'khutu mwake. Imene siimvera liu la oitana, akuchita matsenga mochenjeratu. Thyolani mano ao m'kamwa mwao, Mulungu, zulani zitsakano za misona ya mkango, Yehova. Apitetu ngati madzi oyenda; popiringidza mivi yake ikhale yodukaduka. Apite ngati nkhono yosungunuka; asaone dzuwa monga mtayo. Miphika yanu isanagwire moto waminga, adzaiuluza, yaiwisi ndi yoyaka. Wolungama adzakondwera pakuona kubwezera chilango, adzasamba mapazi ake m'mwazi wa woipa. Ndipo anthu adzati, Indedi, pali mphotho kwa wolungama. Indedi, pali Mulungu wakuweruza pa dziko lapansi. Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Altasheti. Mikitamu wa Davide. Muja Saulo anatuma anthu adikire nyumba yake, kuti amuphe. Ndilanditseni kwa adani anga, Mulungu wanga, ndiikeni pamsanje kwa iwo akundiukira. Mundilanditse kwa ochita zopanda pake, ndipo ndipulumutseni kwa anthu olira mwazi. Pakuti onani, alalira moyo wanga; amphamvu andipangira chiwembu, osachimwa, osalakwa ine, Yehova, osawapatsa chifukwa ine, athamanga nadzikonza. Galamukani kukomana nane, ndipo penyani. Ndinu Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele. Ukani kukazonda amitundu onse, musachitire chifundo mmodzi yense wakuchita zopanda pake monyenga. Abwera madzulo, auwa ngati galu, nazungulira mudzi. Onani abwetuka pakamwa pao; m'milomo mwao muli lupanga, pakuti amati, Amva ndani? Koma Inu, Yehova, mudzawaseka; mudzalalatira amitundu onse. Inu, mphamvu yanga, ndidzakulindirani; pakuti Mulungu ndiye msanje wanga. Mulungu wa chifundo changa adzandichingamira, adzandionetsa tsoka la adani anga. Musawapheretu, angaiwale anthu anga, muwabalalitse mwa mphamvu yanu, ndipo muwagwetse, Ambuye, ndinu chikopa chathu. Pakamwa pao achimwa ndi mau onse a pa milomo yao, potero akodwe m'kudzitamandira kwao, ndiponso chifukwa cha kutemberera ndi bodza azilankhula. Muwathe mumkwiyo, muwagulule psiti. Ndipo adziwe kuti Mulungu ndiye woweruza m'Yakobo, kufikira malekezero a dziko la pansi. Ndipo abwere madzulo, auwe ngati galu, nazungulire mudzi. Ayendeyende ndi kufuna chakudya, nachezere osakhuta. Koma ine, ndidzaimbira mphamvu yanu; inde ndidzaimbitsa chifundo chanu mamawa, pakuti Inu mwakhala msanje wanga, ndi pothawirapo ine tsiku la nsautso yanga. Ndidzaimbira zakukulemekezani Inu, mphamvu yanga; pakuti Mulungu ndiye msanje wanga, Mulungu wa chifundo changa. Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Susan-Eduti. Mikitamu wa Davide; lakulangiza; muja analimbana nao Aramu Naharaimu ndi Aramu Zoba, nabwera Yowabu anapha a Edomu kuchigwa cha Mchere zikwi khumi mphambu ziwiri. Mwatitaya Mulungu, mwatipasula; mwakwiya; tibwezereni. Mwagwedeza dziko, mwaling'amba. Konzani ming'alu yake; pakuti ligwedezeka. Mwaonetsa anthu anu zowawa, mwatimwetsa vinyo wotinjenjemeretsa. Koma mwapatsa mbendera akuopa Inu, aikweze chifukwa cha choonadi. Kuti okondedwa anu alanditsidwe, pulumutsani ndi dzanja lanu lamanja, ndipo mutivomereze. Mulungu walankhula m'chiyero chake; ndidzakondwerera, ndidzagawa Sekemu, ndidzayesa muyeso chigwa cha Sukoti. Giliyadi ndi wanga, Manasenso ndi wanga; ndipo Efuremu ndi mphamvu ya mutu wanga; Yuda ndiye wolamulira wanga. Mowabu ndiye mkhate wanga; pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga. Filistiya, fuulatu chifukwa cha ine. Adzandifikitsa ndani m'mudzi wa m'linga? Adzanditsogolera ndani ku Edomu? Si ndinu, Mulungu, amene mwatitaya? Osatuluka nao makamu athu, Mulungu. Tithandizeni kunsautso; kuti chipulumutso cha munthu ndi chabe. Mwa Mulungu tidzachita molimbika mtima, ndipo Iye adzapondereza otisautsa. Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Neginoto. Salimo la Davide. Imvani mfuu wanga, Mulungu; mverani pemphero langa. Ku malekezero a dziko lapansi ndidzafuulira kwa Inu, pomizika mtima wanga. Nditsogolereni kuthanthwe londiposa ine m'kutalika kwake. Pakuti munakhala pothawirapo panga; nsanja yolimba pothawa mdani ine. Ndidzagoneragonerabe m'chihema mwanu; ndidzathawira mobisalamo m'mapiko anu. Pakuti Inu, Mulungu, mudamva zowinda zanga; munandipatsa cholowa cha iwo akuopa dzina lanu. Mudzatalikitsa moyo wa mfumu. Zaka zake zidzafikira mibadwomibadwo. Adzakhala nthawi zonse pamaso pa Mulungu; mumpatse chifundo ndi choonadi zimsunge. Potero ndidzaimba zolemekeza dzina lanu kunthawi zonse, kuti ndichite zowinda zanga tsiku ndi tsiku. Kwa Mkulu wa Nyimbo, pa Yedutuni, Salimo la Davide. Moyo wanga ukhalira chete Mulungu yekha; chipulumutso changa chifuma kwa Iye. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa; msanje wanga, sindidzagwedezeka kwakukulu. Mudzamvumvulukira munthu mpaka liti, kumupha iye, nonsenu, monga khoma lopendekeka, ndi mpanda woweyeseka? Komatu amkhalira upo kuti amkankhire pansi ulemu wake; akondwera nao mabodza; adalitsa ndi m'kamwa mwao, koma atemberera mumtima. Moyo wanga, ukhalire chete Mulungu yekha; pakuti chiyembekezo changa chifuma kwa Iye. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, msanje wanga, sindidzagwedezeka. Pa Mulungu pali chipulumutso changa ndi ulemerero wanga. Thanthwe la mphamvu yanga ndi pothawirapo panga mpa Mulungu. Khulupirirani pa Iye nyengo zonse, anthu inu, tsanulirani mitima yanu pamaso pake. Mulungu ndiye pothawirapo ife. Indetu, anthu achabe ndi mpweya, ndipo anthu akulu ndi bodza, pakuwayesa apepuka; onse pamodzi apepuka koposa mpweya. Musakhulupirire kusautsa, ndipo musatama chifwamba; chikachuluka chuma musakhazikepo mitima yanu. Mulungu ananena kamodzi, ndinachimva kawiri, kuti mphamvu ndi yake ya Mulungu. Chifundonso ndi chanu, Ambuye, Chifukwa Inu mubwezera munthu aliyense monga mwa ntchito yake. Salimo la Davide; muja anakhala m'chipululu cha Yuda Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga; ndidzakufunani m'matanda kucha. Moyo wanga ukumva ludzu la kwa Inu, thupi langa lilirira Inu, m'dziko louma ndi lotopetsa, lopanda madzi. Kuti ndione mphamvu yanu ndi ulemerero wanu, monga ndinakuonani m'malo oyera. Pakuti chifundo chanu chiposa moyo makomedwe ake; milomo yanga idzakulemekezani. Potero ndidzakuyamikani m'moyo mwanga; ndidzakweza manja anga m'dzina lanu. Mudzakhutitsa moyo wanga ngati ndi mafuta ndi chonona; ndipo pakamwa panga ndidzakulemekezani ndi milomo yakufuula mokondwera. Pokumbukira Inu pa kama wanga, ndi kulingalira za Inu maulonda a usiku. Pakuti munakhala mthandizi wanga; ndipo ndidzafuula mokondwera mu mthunzi wa mapiko anu. Moyo wanga uumirira Inu. Dzanja lamanja lanu lindigwiriziza. Koma iwo amene afuna moyo wanga kuti auononge, adzalowa m'munsi mwake mwa dziko. Adzawapereka kumphamvu ya lupanga; iwo adzakhala gawo la ankhandwe. Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu; yense wakulumbirira iye adzatamandira; pakuti pakamwa pa iwo onena bodza padzatsekedwa. Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide. Imvani Yehova, mau anga, m'kudandaula kwanga; sungani moyo wanga angandiopse mdani. Ndibiseni pa upo wachinsinsi wa ochita zoipa; pa phokoso la ochita zopanda pake. Amene anola lilime lao ngati lupanga, napiringidza mivi yao, ndiyo mau akuwawitsa; kuponyera wangwiro mobisika: Amponyera modzidzimutsa, osaopa. Alimbikitsana m'chinthu choipa; apangana za kutchera misampha mobisika; akuti, Adzaiona ndani? Afunafuna zosalungama; kusanthula, asanthuladi mpaka kutha; chingakhale cha m'kati mwake mwa munthu, ndi mtima wozama. Koma Mulungu adzawaponyera muvi; adzalaswa modzidzimutsa. Adzawakhumudwitsa, lilime lao lidzawatsutsa; onse akuwaona adzawathawa. Ndipo anthu onse adzachita mantha; nadzabukitsa chochita Mulungu, nadzasamalira ntchito yake. Wolungama adzakondwera mwa Yehova, nadzakhulupirira Iye; ndipo oongoka mtima onse adzalemekeza. Kwa Mkulu wa Nyimbo; Salimo la Davide. Nyimbo. M'Ziyoni akulemekezani Inu mwachete, Mulungu, adzakuchitirani Inu chowindachi. Wakumva pemphero Inu, zamoyo zonse zidzadza kwa Inu. Mphulupulu zinandilaka; koma mudzafafaniza zolakwa zathu. Wodala munthuyo mumsankha, ndi kumyandikizitsa, akhale m'mabwalo anu. Tidzakhuta nazo zokoma za m'nyumba yanu, za m'malo oyera a Kachisi wanu. Mudzatiyankha nazo zoopsa m'chilungamo, Mulungu wa chipulumutso chathu; ndinu chikhulupiriko cha malekezero onse a dziko lapansi, ndi cha iwo okhala kutali kunyanja. Ndinu amene mukhazikitsa mapiri ndi mphamvu yanu; pozingidwa nacho chilimbiko. Amene atontholetsa kukuntha kwa nyanja, kukuntha kwa mafunde ake, ndi phokoso la mitundu ya anthu. Ndipo iwo akukhala kumalekezero adzachita mantha chifukwa cha zizindikiro zanu; mukondweretsa apo patulukira dzuwa, ndi apo lilowera. Mucheza nalo dziko lapansi, mulithirira, mulilemeza kwambiri; mtsinje wa Mulungu udzala nao madzi, muwameretsera tirigu m'mene munakonzera nthaka. Mukhutitsa nthaka yake yolima; mufafaniza nthumbira zake; muiolowetsa ndi mvumbi; mudalitsa mmera wake. Muveka chakachi ndi ukoma wanu; ndipo mabande anu akukha zakucha. Akukha pa mabusa a m'chipululu; ndipo mapiri azingika nacho chimwemwe. Podyetsa mpodzaza ndi zoweta; ndipo zigwa zakutidwa ndi tirigu; zifuula mokondwera, inde ziimbira. Kwa Mkulu wa Nyimbo. Nyimbo, Salimo. Fuulirani kwa Mulungu, dziko lonse lapansi. Imbirani ulemerero wa dzina lake; pomlemekeza mumchitire ulemerero. Nenani kwa Mulungu, Ha, ntchito zanu nzoopsa nanga! Chifukwa cha mphamvu yanu yaikulu adani anu adzagonjera Inu. Dziko lonse lapansi lidzakugwadirani, ndipo lidzakuimbirani; ndzaimbira dzina lanu. Idzani, muone ntchito za Mulungu; zochitira Iye ana a anthu nzoopsa. Anasanduliza nyanja ikhale mtunda. Anaoloka mtsinje choponda pansi, apo tinakondwera mwa Iye. Achita ufumu mwa mphamvu yake kosatha; maso ake ayang'anira amitundu; opikisana ndi Iye asadzikuze. Lemekezani Mulungu wathu, mitundu ya anthu inu, ndipo mumveketse liu la chilemekezo chake. Iye amene asunga moyo wathu tingafe, osalola phazi lathu literereke. Pakuti munatiyesera, Mulungu, munatiyenga monga ayenga siliva. Munapita nafe kuukonde; munatisenza chothodwetsa pamsana pathu. Munapititsa anthu oberekeka pamwamba pamitu pathu; tinapyola moto ndi madzi; koma munatifikitsa potitsitsimutsa. Ndidzalowa m'nyumba yanu ndi nsembe zopsereza, ndidzakuchitirani zowinda zanga, zimene inazitchula milomo yanga, ndinazinena pakamwa panga posautsika ine. Ndidzakufukizirani nsembe zopsereza zonona, pamodzi ndi chofukiza cha mphongo za nkhosa; ndidzakonza ng'ombe pamodzi ndi mbuzi. Idzani, imvani, inu nonse akuopa Mulungu, ndipo ndidzafotokozera zonse anazichitira moyo wanga. Ndinamfuulira Iye pakamwa panga, ndipo ndinamkuza ndi lilime langa. Ndikadasekera zopanda pake m'mtima mwanga, Ambuye sakadamvera. Koma Mulungu anamvadi; anamvera mau a pemphero langa. Wolemekezeka Mulungu, amene sanandipatutsire ine pemphero langa, kapena chifundo chake. Kwa Mkulu wa Nyimbo, pa Neginoto. Salimo, Nyimbo. Atichitire chifundo Mulungu, ndi kutidalitsa, atiwalitsire nkhope yake; kuti njira yanu idziwike pa dziko lapansi, chipulumutso chanu mwa amitundu onse. Anthu akuyamikeni, Mulungu; anthu onse akuyamikeni. Anthu akondwere, nafuule mokondwera; pakuti mudzaweruza anthu molunjika, ndipo mudzalangiza anthu pa dziko lapansi. Anthu akuyamikeni, Mulungu; anthu onse akuyamikeni. Dziko lapansi lapereka zipatso zake, Mulungu, Mulungu wathu adzatidalitsa. Mulungu adzatidalitsa; ndipo malekezero onse a dziko lapansi adzamuopa Iye. Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide. Nyimbo. Auke Mulungu, abalalike adani ake; iwonso akumuda athawe pamaso pake. Muwachotse monga utsi uchotseka; monga phula lisungunuka pamoto, aonongeke oipa pamaso pa Mulungu. Koma olungama akondwere; atumphe ndi chimwemwe pamaso pa Mulungu; ndipo asekere nacho chikondwerero. Imbirani Yehova, liimbireni nyimbo dzina lake; undirani mseu Iye woberekekayo kuchidikha; dzina lake ndiye Yehova; ndipo tumphani ndi chimwemwe pamaso pake. Mulungu, mokhala mwake moyera, ndiye Atate wa ana amasiye, ndi woweruza wa akazi amasiye. Mulungu amangitsira banja anthu a pa okha; atulutsa am'ndende alemerere; koma opikisana naye akhala m'dziko lopanda madzi. Pakutuluka paja, Inu Mulungu, ndi kutsogolera anthu anu, pakuyenda paja Inu m'chipululu. Dziko lapansi linagwedezeka, inde thambo linakha pamaso pa Mulungu; Sinai lomwe linagwedezeka pamaso pa Mulungu, Mulungu wa Israele. Inu, Mulungu, munavumbitsa chimvula, munatsitsimutsa cholowa chanu pamene chidathodwa. Gulu lanu linakhala m'dziko muja. Mwa ukoma wanu munalikonzera ozunzika, Mulungu. Ambuye anapatsa mau, akazi akulalikira uthengawo ndiwo khamu lalikulu. Mafumu a magulu a ankhondo athawathawa, ndipo mkazi amene akhala kwao agawa zofunkha. Pogona inu m'makola a zoweta, mukhala ngati mapiko a njiwa okulira ndi siliva, ndi nthenga zake zokulira ndi golide woyenga wonyezimira. Pamene Wamphamvuyonse anabalalitsa mafumu m'dzikomo, munayera ngati matalala m'Zalimoni. Phiri la Basani ndilo phiri la Mulungu; Phiri la Basani ndilo phiri la mitumitu. Muchitiranji nsanje mapiri inu a mitumitu, ndi phirilo Mulungu analikhumba, akhaleko? Inde, Yehova adzakhalabe komweko kosatha. Magaleta a Mulungu ndiwo zikwi makumi awiri, inde zikwi zowirikizawirikiza, Ambuye ali pakati pao, monga m'Sinai, m'malo opatulika. Munakwera kunka kumwamba, munapita nao undende kuuyesa ndende; munalandira zaufulu mwa anthu, ngakhale mwa opikisana nanu, kuti Yehova Mulungu akakhale nao. Wolemekeza Ambuye, tsiku ndi tsiku atisenzera katundu, ndiye Mulungu wa chipulumutso chathu. Mulungu akhala kwa ife Mulungu wa chipulumutso; ndipo Yehova Ambuye ali nazo zopulumutsira kuimfa. Indedi Mulungu adzaphwanya mutu wa adani ake, pakati pa mutu pa iye woyendabe m'kutsutsika kwake. Ambuye anati, Ndidzawatenganso ku Basani, ndidzawatenganso kozama kwa nyanja, kuti uviike phazi lako m'mwazi, kuti malilime a agalu ako alaweko adani ako. Anapenya mayendedwe anu, Mulungu, mayendedwe a Mulungu wanga, mfumu yanga, m'malo oyera. Oimbira anatsogolera, oimba zoimba anatsata m'mbuyo, pakatipo anamwali oimba mangaka. Lemekezani Mulungu m'masonkhano, ndiye Ambuye, inu a gwero la Israele. Apo pali Benjamini wamng'ono, wakuwachita ufumu, akulu a Yuda, ndi a upo wao, akulu a Zebuloni, akulu a Nafutali. Mulungu wako analamulira mphamvu yako, Limbitsani, Mulungu, chimene munatichitira. Chifukwa cha Kachisi wanu wa m'Yerusalemu mafumu adzabwera nacho chaufulu kukupatsani. Dzudzulani chilombo cha m'bango, khamu la mphongo ndi ng'ombe za anthu, yense wakudzigonjera ndi ndalama za siliva; anabalalitsa mitundu ya anthu ya kukondwera nayo nkhondo. Akulu adzafumira ku Ejipito; Kusi adzafulumira kutambalitsa manja ake kwa Mulungu. Imbirani Mulungu, maufumu a dziko lapansi inu; imbirani Ambuye zomlemekeza. Kwa Iye wakuberekeka pamwambamwamba, oyambira kale lomwe; taonani; amveketsa liu lake, ndilo liu lamphamvu. Vomerezani kuti mphamvu nja Mulungu; ukulu wake uli pa Israele, ndi mphamvu yake m'mitambo. Inu Mulungu, ndinu woopsa m'malo oyera anu; Mulungu wa Israele ndiye amene apatsa anthu ake mphamvu ndi chilimbiko. Alemekezeke Mulungu. Kwa Mkulu wa Nyimbo. Pa Syosyanimu. Salimo la Davide. Ndipulumutseni Mulungu; pakuti madzi afikira moyo wanga. Ndamira m'thope lozama, lopanda poponderapo; ndalowa m'madzi ozama, ndipo chigumula chandimiza. Ndalema ndi kufuula kwanga; kum'mero kwauma gwa! M'maso mwanga mwada poyembekeza Mulungu wanga. Ondida kopanda chifukwa achuluka koposa tsitsi la pamutu panga; ofuna kunditha, ndiwo adani anga monama, ali ndi mphamvu. Pamenepo andibwezetsa chosafunkha ine. Mulungu, mudziwa kupusa kwanga; ndipo kutsutsika kwanga sikubisikira Inu. Iwo akuyembekeza Inu, Ambuye Yehova wa makamu, asachite manyazi chifukwa cha ine, iwo ofuna Inu, Mulungu wa Israele, asapepulidwe chifukwa cha ine. Pakuti ndalola chotonza chifukwa cha Inu, chimpepulo chakuta nkhope yanga. Abale anga andiyesa mlendo, ndi ana a mai wanga andiyesa wa mtundu wina. Pakuti changu cha pa nyumba yanu chandidya; ndi zotonza za iwo otonza Inu zandigwera ine. Ndipo ndinalira pa kusala kwa moyo wanga, koma uku kunandikhalira chotonza. Ndipo chovala changa ndinayesa chiguduli, koma amandiphera mwambi. Okhala pachipata akamba za ine; ndipo oledzera andiimba. Koma ine, pemphero langa lili kwa Inu, Yehova, m'nyengo yolandirika; Mulungu, mwa chifundo chanu chachikulu, mundivomereze ndi choonadi cha chipulumutso chanu. Mundilanditse kuthope, ndisamiremo, ndilanditseni kwa iwo akundida, ndi kwa madzi ozama. Chigumula chisandifotsere, ndipo chakuya chisandimize; ndipo asanditsekere pakamwa pake pa dzenje. Mundiyankhe Yehova; pakuti chifundo chanu nchokoma; munditembenukire monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu. Ndipo musabisire nkhope yanu mtumiki wanu; pakuti ndisautsika ine; mundiyankhe msanga. Yandikizani moyo wanga, ndi kuuombola; ndipulumutseni chifukwa cha adani anga. Mudziwa chotonza changa, ndi manyazi anga, ndi chimpepulo changa. Akundisautsa ali pamaso panu. Chotonza chandiswera mtima, ndipo ndidwala ine; ndipo ndinayembekeza wina wondichitira chifundo, koma palibe; ndinayembekeza onditonthoza mtima, osawapeza. Ndipo anandipatsa ndulu ikhale chakudya changa; nandimwetsa vinyo wosasa pomva ludzu ine. Gome lao likhale msampha pamaso pao; pokhala ndi mtendere iwo, likhale khwekhwe. M'maso mwao mude, kuti asapenye; ndipo munjenjemeretse m'chuuno mwao kosalekeza. Muwatsanulire mkwiyo wanu, ndipo moto wa ukali wanu uwagwere. Pokhala pao pakhale bwinja; m'mahema mwao musakhale munthu. Pakuti alondola amene Inu munampanda; ndipo akambirana za zowawa zao za iwo amene munawalasa. Onjezani mphulupulu pa mphulupulu zao; ndipo asafikire chilungamo chanu. Afafanizidwe m'buku lamoyo, ndipo asalembedwe pamodzi ndi olungama. Koma ine ndine wozunzika ndi womva zowawa; chipulumutso chanu, Mulungu, chindikweze pamsanje. Ndidzalemekeza dzina la Mulungu ndi kuliimbira, ndipo ndidzambukitsa ndi kumyamika. Ndipo chidzakomera Yehova koposa ng'ombe, inde mphongo za nyanga ndi ziboda. Ofatsa anachiona, nakondwera, ndipo inu, ofuna Mulungu, mtima wanu ukhale ndi moyo. Pakuti Yehova amvera aumphawi, ndipo sapeputsa am'ndende ake. Zakumwamba ndi dziko lapansi zimlemekeze, nyanja ndi zonse zoyenda m'mwemo. Pakuti Mulungu adzapulumutsa Ziyoni, nadzamanga midzi ya Yuda; ndipo iwo adzakhala komweko, likhale laolao. Ndipo mbumba ya atumiki ake idzalilandira; ndipo iwo akukonda dzina lake adzakhala m'mwemo. Kwa Mkulu wa Nyimbo; Salimo la Davide, la chikumbutso. Fulumirani kundipulumutsa, Mulungu! Fulumirani kundithandiza, Yehova. Achite manyazi, nadodome amene afuna moyo wanga. Abwezedwe m'mbuyo, napepulidwe amene akonda kundichitira choipa. Abwerere, kukhale mphotho ya manyazi ao amene akuti, Hede, hede. Asekerere nakondwerere mwa Inu onse akufuna Inu; nanene kosalekeza iwo akukonda chipulumutso chanu, abuke Mulungu. Koma ine ndine wozunzika ndi waumphawi; mundifulumirire, Mulungu. Inu ndinu mthandizi wanga ndi Mpulumutsi wanga; musachedwe, Yehova. Ndikhulupirira Inu, Yehova. Ndisachite manyazi nthawi zonse. Ndikwatuleni m'chilungamo chanu, ndi kundilanditsa, nditcherereni khutu lanu ndi kundipulumutsa. Mundikhalire thanthwe lokhalamo, lopitako kosaleka; mwalamulira kundipulumutsa; popeza Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa. Ndilanditseni, Mulungu wanga, m'dzanja la woipa, m'dzanja la munthu wosalungama ndi wachiwawa. Pakuti Inu ndinu chiyembekezo changa, Ambuye Yehova; mwandikhalira wokhulupirika kuyambira ubwana wanga. Inu munandigwiriziza kuyambira ndisanabadwe, kuyambira pa thupi la mai wanga wondichitira zokoma ndinu; ndidzakulemekezani kosalekeza. Ndikhala chodabwitsa kwa ambiri; koma Inu ndinu pothawira panga polimba. M'kamwa mwanga mudzadzala lemekezo lanu, ndi ulemu wanu tsiku lonse. Musanditaye mu ukalamba wanga; musandisiye, pakutha mphamvu yanga. Pakuti adani anga alankhula za ine; ndipo iwo akulalira moyo wanga apangana upo, ndi kuti, Wamsiya Mulungu. Mlondoleni, mgwireni; popeza palibe wompulumutsa. Musandikhalire kutali, Mulungu; fulumirani kundithandiza, Mulungu. Adani a moyo wanga achite manyazi, nathawe; chotonza ndi chimpepulo zikute ondifunira choipa. Koma ine ndidzayembekeza kosaleka, ndipo ndidzaonjeza kukulemekezani. Pakamwa panga padzafotokozera chilungamo chanu, ndi chipulumutso chanu tsiku lonse; pakuti sindidziwa mawerengedwe ake. Ndidzamuka mu mphamvu ya Ambuye Yehova; ndidzatchula chilungamo chanu, inde chanu chokha. Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ubwana wanga; ndipo kufikira lero ndilalikira zodabwitsa zanu. Poteronso pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu; kufikira nditalalikira mbadwo uwu za dzanja lanu, mphamvu yanu kwa onse akudza m'mbuyo. Chilungamo chanunso, Mulungu, chifikira kuthambo; Inu amene munachita zachikulu, akunga Inu ndani, Mulungu? Inu, amene munationetsa nsautso zambiri ndi zoipa, mudzatipatsanso moyo, ndi kutitenganso munsi mwa dziko. Mundionjezere ukulu wanga, ndipo munditembenukire kundisangalatsa. Ndiponso ndidzakuyamikani ndi chisakasa, kubukitsa choonadi chanu, Mulungu wanga; ndidzakuimbirani nyimbo ndi zeze, ndinu Woyerayo wa Israele. Milomo yanga idzafuula mokondwera poimbira Inu nyimbo; inde, moyo wanga umene munaombola. Lilime langa lomwe lidzalankhula za chilungamo chanu tsiku lonse, pakuti ofuna kundichitira choipa achita manyazi, nadodoma. Salimo la kwa Solomoni. Patsani mfumu maweruzo anu, Mulungu, ndi mwana wa mfumu chilungamo chanu. Potero adzanenera anthu anu mlandu ndi m'chilungamo, ndi ozunzika anu ndi m'chiweruzo. Mapiri adzatengera anthu mtendere, timapiri tomwe, m'chilungamo. Adzaweruza ozunzika a mwa anthu, adzapulumutsa ana aumphawi, nadzaphwanya wosautsa. Adzakuopani momwe likhalira dzuwa ndi mwezi, kufikira mibadwomibadwo. Adzanga mvula yakugwa pa udzu wosenga, monga mvula yothirira dziko. Masiku ake wolungama adzakhazikika; ndi mtendere wochuluka, kufikira sipadzakhala mwezi. Ndipo adzachita ufumu kuchokera kunyanja kufikira kunyanja, ndi kuchokera ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko lapansi. Okhala m'chipululu adzagwadira pamaso pake; ndi adani ake adzaluma nthaka. Mafumu a ku Tarisisi ndi ku Zisumbuzo adzabwera nacho chopereka; mafumu a ku Sheba ndi Seba adzadza nazo mphatso. Inde mafumu onse adzamgwadira iye, amitundu onse adzamtumikira. Pakuti adzapulumutsa waumphawi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphawi, nadzapulumutsa moyo wa aumphawi. Adzaombola moyo wao ku chinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wao udzakhala wa mtengo pamaso pake. Ndipo iye adzakhala ndi moyo; ndipo adzampatsa golide wa ku Sheba; nadzampempherera kosalekeza; adzamlemekeza tsiku lonse. M'dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri; zipatso zake zidzati waa, ngati za ku Lebanoni, ndipo iwo a m'mudzi adzaphuka ngati msipu wapansi. Dzina lake lidzakhala kosatha, momwe likhalira dzuwa dzina lake lidzamvekera zidzukulu. Ndipo anthu adzadalitsidwa mwa Iye; amitundu onse adzamutcha wodala. Wolemekezeka Yehova Mulungu, Mulungu wa Israele, amene achita zodabwitsa yekhayo. Ndipo dzina lake la ulemerero lidalitsike kosatha; ndipo dziko lonse lapansi lidzale nao ulemerero wake. Amen, ndi Amen. Mapemphero a Davide mwana wa Yese atha. Salimo la Asafu. Indedi Mulungu achitira Israele zabwino, iwo a mtima wa mbee. Koma ine, ndikadagwa; mapazi anga akadaterereka. Pakuti ndinachitira nsanje odzitamandira, pakuona mtendere wa oipa. Pakuti palibe zomangira pakufa iwo, ndi mphamvu yao njolimba. Savutika monga anthu ena; sasautsika monga anthu ena. Chifukwa chake kudzikuza kunga unyolo pakhosi pao; achivala chiwawa ngati malaya. Kunenepa kwao kutuzulitsa maso ao, malingaliro a mitima yao asefukira. Achita zaphwete nalankhula moipa za kusautsa, alankhula modzitama. Pakamwa pao anena zam'mwamba, ndipo lilime lao liyendayenda m'dziko lapansi. Chifukwa chake anthu ake amabwera kudza kuno, ndipo chikho chodzala ndi madzi achigugudiza. Namati, Akachidziwa bwanji Mulungu? Kodi Wam'mwambamwamba ali nayo nzeru? Tapenyani, oipa ndi awa; ndipo pokhazikika chikhazikikire aonjezerapo pa chuma chao. Indedi, ndinayeretsa mtima wanga kwachabe, ndipo ndinasamba m'manja mosalakwa. Popeza andisautsa tsiku lonse, nandilanga mamawa monse, ndikadati, Ndidzafotokozera chotere, taonani, ndikadachita chosakhulupirika ndi mbadwo wa ana ako. Pamene ndinayesa kudziwitsa ichi, ndinavutika nacho; mpaka ndinalowa m'zoyera za Mulungu, ndi kulingalira chitsiriziro chao. Indedi muwaika poterera, muwagwetsa kuti muwaononge. Ha? M'kamphindi ayesedwa bwinja; athedwa konse ndi zoopsa. Monga anthu atauka, apepula loto; momwemo, Inu Ambuye, pakuuka mudzapeputsa chithunzithunzi chao. Pakuti mtima wanga udawawa, ndipo ndinalaswa m'impso zanga; ndinali wam'thengo, wosadziwa kanthu; ndinali ngati nyama pamaso panu. Koma ndikhala ndi Inu chikhalire, mwandigwira dzanja langa la manja. Mudzanditsogolera ndi uphungu wanu, ndipo mutatero, mudzandilandira m'ulemerero. Ndili ndi yani Kumwamba, koma Inu? Ndipo pa dziko lapansi palibe wina wondikonda koma Inu. Likatha thupi langa ndi mtima wanga, Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga, ndi cholandira changa chosatha. Pakuti, taonani, iwo okhala patali ndi Inu adzaonongeka; muononga onse akupembedza kwina, kosiyana ndi Inu. Koma ine, kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu. Ndimuyesa Ambuye Yehova pothawirapo ine, kuti ndifotokozere ntchito zanu zonse. Chilangizo cha Asafu. Mulungu, munatitayiranji chitayire? Mkwiyo wanu ufukiranji pa nkhosa za kubusa kwanu? Kumbukirani msonkhano wanu, umene munaugula kale, umene munauombola ukhale fuko la cholandira chanu; Phiri la Ziyoni limene mukhalamo. Nyamulani mapazi anu kukapenya mapasukidwe osatha, zoipa zonse adazichita mdani m'malo opatulika. Otsutsana ndi Inu abangula pakati pa msonkhano wanu; aika mbendera zao zikhale zizindikiro. Anaoneka ngati osamula nkhwangwa kunkhalango. Ndipo tsopano aphwanya zosemeka zake zonse ndi nkhwangwa ndi nyundo. Anatentha malo anu opatulika; anaipsa ndi kugwetsa pansi mokhalamo dzina lanu. Ananena mumtima mwao, Tiwapasule pamodzi; anatentha zosonkhaniramo za Mulungu zonse, m'dzikomo. Sitiziona zizindikiro zathu; palibenso mneneri; ndipo mwa ife palibe wina wakudziwa mpaka liti. Wotsutsanayo adzatonza kufikira liti, Mulungu? Kodi mdani adzanyoza dzina lanu nthawi yonse? Mubwezeranji dzanja lanu, ndilo dzanja lamanja lanu? Mulitulutse kuchifuwa chanu ndipo muwatheretu. Koma Mulungu ndiye mfumu yanga kuyambira kale, wochita zakupulumutsa pakati pa dziko lapansi. Mudagawa nyanja ndi mphamvu yanu; mudaswa mitu ya zoopsa za m'madzi. Mudaphwanya mitu ya Leviyatani; mudampereka akhale chakudya cha zilombo za m'chipululu. Mudagawa kasupe ndi mtsinje; mudaphwetsa mitsinje yaikulu. Usana ndi wanu, usikunso ndi wanu, munakonza kuunika ndi dzuwa. Munaika malekezero onse a dziko lapansi; munalenga dzinja ndi malimwe. Mukumbukire ichi, Yehova, mdaniyo anatonza, ndipo anthu opusa ananyoza dzina lanu. Musapereke moyo wa njiwa yanu kwa chilombo; musamaiwala moyo wa ozunzika anu nthawi yonse. Samalirani chipanganocho; pakuti malo a mdima a m'dziko adzala ndi zokhalamo chiwawa. Okhalira mphanthi asabwere nao manyazi; wozunzika ndi waumphawi alemekeze dzina lanu. Nyamukani, Mulungu, mudzinenere mlandu nokha; kumbukirani momwe akutonzani wopusa tsiku lonse. Musaiwale mau a iwo otsutsana ndi Inu; kusokosera kwa iwo akuukirani Inu kumakwera kosaleka. Kwa Mkulu wa Nyimbo; Altasyeti; Salimo la Asafu. Nyimbo. Tikuyamikani Inu, Mulungu; tiyamika, pakuti dzina lanu lili pafupi; afotokozera zodabwitsa zanu. Pakuona nyengo yake ndidzaweruza molunjika. Lasungunuka dziko lapansi, ndi onse okhalamo; ndinachirika mizati yake. Ndinati kwa odzitamandira, musamachita zodzitamandira; ndi kwa oipa, Musamakweza nyanga; musamakwezetsa nyanga yanu; musamalankhula ndi khosi louma. Pakuti kukuzaku sikuchokera kum'mawa, kapena kumadzulo, kapena kuchipululu. Pakuti Mulungu ndiye woweruza; achepsa wina, nakuza wina. Pakuti m'dzanja la Yehova muli chikho; ndi vinyo wake achita thovu; chidzala ndi zosanganizira, ndipo atsanulako. Indedi, oipa onse a pa dziko lapansi adzamwa nadzagugudiza nsenga zake. Koma ine ndidzalalikira kosalekeza, ndidzaimbira zomlemekeza Mulungu wa Yakobo. Ndipo ndidzatseteka nyanga zonse za oipa; koma nyanga za wolungama zidzakwezeka. Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Neginoto. Salimo la Asafu. Nyimbo. Mulungu adziwika mwa Yuda, dzina lake limveka mwa Israele. Msasa wake unali m'Salemu, ndipo pokhala Iye m'Ziyoni. Pomwepo anathyola mivi ya pauta; chikopa, ndi lupanga, ndi nkhondo. Inu ndinu wakuunikira, ndi womveka wakuposa mapiri muli achifwamba. Olimba mtima chifunkhidwa chuma chao, agona tulo tao; amuna onse amphamvu asowa manja ao. Pa kudzudzula kwanu, Mulungu wa Yakobo, galeta ndi kavalo yemwe anagwa m'tulo. Inu ndinu woopsa; ndipo utauka mkwiyo wanu adzakhala chilili ndani pamaso panu? Mudamveketsa chiweruzo chochokera Kumwamba; dziko lapansi linachita mantha, nilinakhala chete, pakuuka Mulungu kuti aweruze, kuti apulumutse ofatsa onse a pa dziko lapansi. Indedi, kuzaza kwake kwa munthu kudzakulemekezani; chotsalira cha kuzazaku mudzachiletsa. Windani ndipo chitirani Yehova Mulungu wanu zowindazo; onse akumzinga abwere nacho chopereka cha kwa Iye amene ayenera kumuopa. Iye adzadula mzimu wa akulu; akhala woopsa kwa mafumu a pa dziko lapansi. Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Yedutuni; Salimo la Asafu. Ndidzafuulira kwa Mulungu ndi mau anga; kwa Mulungu ndi mau anga, ndipo adzanditcherezera khutu. Tsiku la nsautso yanga ndinafuna Ambuye. Dzanja langa linatambalika usiku, losaleka; mtima wanga unakana kutonthozedwa. Ndikumbukira Mulungu ndipo ndivutika; ndilingalira ndipo mzimu wanga ukomoka. Mundikhalitsa maso; ndigwidwa mtima wosanena kanthu. Ndinaganizira masiku akale, zaka zakalekale. Ndikumbukira nyimbo yanga usiku; ndilingalira mumtima mwanga; mzimu wanga unasanthula. Kodi Ambuye adzataya nthawi yonse? Osabwerezanso kukondwera nafe. Chifundo chake chalekeka konsekonse kodi? Lonjezano lake lidatha kodi ku mibadwo yonse? Kodi Mulungu waiwala kuchita chifundo? Watsekereza kodi nsoni zokoma zake mumkwiyo? Ndipo ndinati, Chindilaka ichi; koma ndikumbukira zaka za dzanja lamanja la Wam'mwambamwamba. Ndidzakumbukira zimene adazichita Yehova; inde, ndidzakumbukira zodabwitsa zanu zoyambira kale. Ndipo ndidzalingalira ntchito yanu yonse, ndi kulingalirabe zimene munazichita Inu. Mulungu, m'malo opatulika muli njira yanu; Mulungu wamkulu ndani monga Mulungu? Inu ndinu Mulungu wakuchita chodabwitsa; munazindikiritsa mphamvu yanu mwa mitundu ya anthu. Munaombola anthu anu ndi mkono wanu, ndiwo ana a Yakobo, ndi a Yosefe. Madziwo anakuonani Mulungu; anakuonani madziwo; anachita mantha, zozama zomwe zinanjenjemera. Makongwa anatsanula madzi; thambo lidamvetsa liu lake; mivi yanu yomwe inatulukira. Liu la bingu lanu linatengezanatengezana; mphezi zinaunikira ponse pali anthu; dziko lapansi linanjenjemera ndi kugwedezeka. Njira yanu inali m'nyanja, koyenda Inu nku madzi aakulu, ndipo mapazi anu sanadziwike. Munatsogolera anthu anu ngati gulu la nkhosa, ndi dzanja la Mose ndi Aroni. Chilangizo cha Asafu. Tamverani, anthu anga, chilamulo changa; tcherezani khutu lanu mau a pakamwa panga. Ndidzatsegula pakamwa panga mofanizira; ndidzatchula zinsinsi zoyambira kale. Zimene tinazimva, ndi kuzidziwa, ndipo makolo athu anatifotokozera. Sitidzazibisira ana ao, koma kufotokozera mbadwo ukudzawo zolemekeza za Yehova, ndi mphamvu yake, ndi zodabwitsa zake zimene anazichita. Anakhazika mboni mwa Yakobo, naika chilamulo mwa Israele, ndizo analamulira atate athu, akazidziwitse ana ao; kuti mbadwo ukudzawo udziwe, ndiwo ana amene akadzabadwa; amene adzaimirira nadzafotokozera ana ao. Ndi kuti chiyembekezo chao chikhale kwa Mulungu, osaiwala zochita Mulungu, koma kusunga malamulo ake ndiko. Ndi kuti asange makolo ao, ndiwo mbadwo woukirana ndi wopikisana ndi Mulungu; mbadwo wosakonza mtima wao, ndi mzimu wao sunakhazikika ndi Mulungu. Ana a Efuremu okhala nazo zida, oponya nao mauta, anabwerera m'mbuyo tsiku la nkhondo. Sanasunga chipangano cha Mulungu, nakana kuyenda m'chilamulo chake. Ndipo anaiwala zochita Iye, ndi zodabwitsa zake zimene anawaonetsa. Anachita chodabwitsa pamaso pa makolo ao, m'dziko la Ejipito kuchidikha cha Zowani. Anagawa nyanja nawapititsapo; naimitsa madziwo ngati khoma. Ndipo msana anawatsogolera ndi mtambo ndi usiku wonse ndi kuunika kwa moto. Anang'alula thanthwe m'chipululu, ndipo anawamwetsa kochuluka monga m'madzi ozama. Anatulukitsa mitsinje m'thanthwe, inde anatsikitsa madzi ngati mitsinje. Koma anaonjeza kumchimwira Iye, kupikisana ndi Wam'mwambamwamba m'chipululu. Ndipo anayesa Mulungu mumtima mwao ndi kupempha chakudya monga mwa kulakalaka kwao. Ndipo analankhula motsutsana ndi Mulungu; anati, Kodi Mulungu akhoza kutikonzera podyera m'chipululu? Taonani, anapanda thanthwe, ndi madzi anayendako ndi mitsinje inasefuka; kodi adzakhozanso kupatsa mkate? Kodi adzafunira anthu ake nyama? Chifukwa chake Yehova anamva, nakwiya; ndipo anayatsa moto pa Yakobo, ndiponso mkwiyo unakwera pa Israele. Popeza sanakhulupirire Mulungu, osatama chipulumutso chake. Koma analamulira mitambo ili m'mwamba, natsegula m'makomo a kumwamba. Ndipo anawavumbitsira mana, adye, nawapatsa tirigu wa kumwamba. Yense anadya mkate wa angelo, anawatumizira chakudya chofikira. Anaombetsa m'mwamba mphepo ya kum'mawa, natsogoza mwera ndi mphamvu yake. Ndipo anawavumbitsira nyama ngati fumbi, ndi mbalame zouluka ngati mchenga wa kunyanja. Ndipo anazigwetsa pakati pa misasa yao, pozungulira pokhala iwo. Potero anadya nakhuta kwambiri; ndipo anawapatsa chokhumba iwo. Asanathe nacho chokhumba chao, chakudya chao chili m'kamwa mwao, pamenepo mkwiyo wa Mulungu unawaukira, ndipo anapha mwa onenepa ao, nagwetsa osankhika a Israele. Chingakhale ichi chonse anachimwanso, osavomereza zodabwitsa zake. Potero anathera masiku ao ndi zopanda pake, ndi zaka zao mwa mantha. Pamene anawapha ndipo anamfuna Iye; nabwerera, nafunitsitsa Mulungu. Ndipo anakumbukira kuti Mulungu ndiye thanthwe lao, ndi Mulungu Wam'mwambamwamba Mombolo wao. Koma anamsyasyalika pakamwa pao, namnamiza ndi lilime lao. Popeza mtima wao sunakonzekera Iye, ndipo sanakhazikike m'chipangano chake. Koma Iye pokhala ngwa chifundo, anakhululukira choipa, osawaononga; nabweza mkwiyo wake kawirikawiri, sanautse ukali wake wonse. Ndipo anakumbukira kuti iwo ndiwo anthu; mphepo yopita yosabweranso. Kawirikawiri nanga anapikisana ndi Iye kuchigwako, nammvetsa chisoni m'chipululu. Pakuti anabwerera m'mbuyo, nayesa Mulungu, nachepsa Woyerayo wa Israele. Sanakumbukire dzanja lake, tsikuli anawaombola kwa msautsi. Amene anaika zizindikiro zake m'Ejipito, ndi zodabwitsa zake kuchidikha cha Zowani. Nasanduliza nyanja yao mwazi, ndi mitsinje yao, kuti sangakhoze kumwa. Anawatumizira pakati pao mitambo ya ntchentche zakuwatha; ndi achule akuwaononga. Ndipo anapatsa mphuchi dzinthu dzao, ndi dzombe ntchito yao. Anapha mphesa zao ndi matalala, ndi mikuyu yao ndi chisanu. Naperekanso zoweta zao kwa matalala, ndi ng'ombe zao kwa mphezi. Anawatumizira mkwiyo wake wotentha, kuzaza, ndi kupsa mtima, ndi nsautso, ndizo gulu la amithenga ochita zoipa. Analambulira mkwiyo wake njira; sanalekerere moyo wao usafe, koma anapereka moyo wao kumliri. Ndipo anapha ana oyamba onse a mu Ejipito, ndiwo oyamba a mphamvu yao m'mahema a Hamu. Koma anatulutsa anthu ake ngati nkhosa, nawatsogoza ngati gulu la zoweta m'chipululu. Ndipo anawatsogolera mokhulupirika, kotero kuti sanaope; koma nyanja inamiza adani ao. Ndipo anawafikitsa kumalire a malo ake oyera, kuphiri ili, dzanja lamanja lake lidaligula. Ndipo anapirikitsa amitundu pamaso pao, nawagawira cholowa chao, ndi muyeso, nakhalitsa mafuko a Israele m'mahema mwao. Koma anamuyesa napikisana ndi Mulungu Wam'mwambamwamba, osasunga mboni zake; koma anabwerera m'mbuyo, nachita zosakhulupirika monga makolo ao, anapatuka ngati uta wolenda. Ndipo anautsa mtima wake ndi malo amsanje ao, namchititsa nsanje ndi mafano osema. Pakumva ichi Mulungu, anakwiya, nanyozatu Israele; ndipo anachokera chokhalamo cha ku Silo, chihemacho adachimanga mwa anthu; napereka mphamvu yake m'ukapolo, ndi ulemerero wake m'dzanja la msautsi. Naperekanso anthu ake kwa lupanga; nakwiya nacho cholandira chake. Moto unapsereza anyamata ao; ndi anamwali ao sanalemekezeke. Ansembe ao anagwa ndi lupanga; ndipo amasiye ao sanachite maliro. Pamenepo Ambuye anauka ngati wam'tulo; ngati chiphona chakuchita nthungululu ndi vinyo. Ndipo anapanda otsutsana naye kumbuyo; nawapereka akhale otonzeka kosatha. Tero anakana hema wa Yosefe; ndipo sanasankhe fuko la Efuremu; koma anasankha fuko la Yuda, Phiri la Ziyoni limene analikonda. Ndipo anamanga malo oyera ake ngati kaphiri, monga dziko lapansi limene analikhazikitsa kosatha. Ndipo anasankha Davide mtumiki wake, namtenga kumakola a nkhosa. Anamtenga kuja anatsata zoyamwitsa, awete Yakobo, anthu ake, ndi Israele, cholandira chake. Potero anawaweta monga mwa mtima wake wangwiro; nawatsogolera ndi luso la manja ake. Salimo la Asafu. Mulungu, akunja alowa m'cholandira chanu; anaipsa Kachisi wanu woyera; anachititsa Yerusalemu bwinja. Anapereka mitembo ya atumiki anu ikhale chakudya cha mbalame za mlengalenga, nyama ya okondedwa anu anaipereka kwa zilombo za m'dziko. Anakhetsa mwazi wao ngati madzi pozungulira Yerusalemu; ndipo panalibe wakuwaika. Takhala chotonza cha anansi athu, ndi choseketsa ndi cholalatitsa iwo akutizinga. Yehova, mudzakwiya nthawi zonse kufikira liti? Nidzatentha nsanje yanu ngati moto? Thirirani mkwiyo wanu pa akunja osadziwa Inu, ndi pa maufumu osaitana pa dzina lanu. Pakuti anathera Yakobo, napasula pokhalira iye. Musakumbukire motitsutsa mphulupulu za makolo athu; nsoni zokoma zanu zitipeze msanga, pakuti tafooka kwambiri. Tithandizeni Mulungu wa chipulumutso chathu, chifukwa cha ulemerero wa dzina lanu; ndipo tilanditseni, ndi kutifafanizira zoipa zathu, chifukwa cha dzina lanu. Anenerenji amitundu, Ali kuti Mulungu wao? Kubwezera chilango cha mwazi wa atumiki anu umene anaukhetsa kudziwike pakati pa amitundu pamaso pathu. Kubuula kwa wandende kufike kuli Inu; monga mwa mphamvu yanu yaikulu lolani ana a imfa atsale. Ndipo anansi athu amene anatonza Inu muwabwezere chotonza chao, kasanu ndi kawiri kumtima kwao, Ambuye. Potero ife anthu anu ndi nkhosa zapabusa panu tidzakuyamikani kosatha; tidzafotokozera chilemekezo chanu ku mibadwomibadwo. Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Syosyanimu; lochita mboni; Salimo la Asafu. Mbusa wa Israele, tcherani khutu; inu wakutsogolera Yosefe ngati nkhosa; inu wokhala pa akerubi, walitsani. Utsani chamuna chanu pamaso pa Efuremu ndi Benjamini ndi Manase, ndipo mutidzere kutipulumutsa. Mutibweze, Mulungu; nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka. Yehova, Mulungu wa makamu, mudzakwiyira pemphero la anthu anu kufikira liti? Munawadyetsa mkate wa misozi, ndipo munawamwetsa misozi yambiri. Mutiika kuti atilimbirane anzathu; ndipo adani athu atiseka mwa iwo okha. Mulungu wa makamu, mutibweze; nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka. Mudatenga mpesa kuchokera ku Ejipito, munapirikitsa amitundu ndi kuuoka uwu. Mudasoseratu pookapo, idagwiritsa mizu yake, ndipo unadzaza dziko. Mthunzi wake unaphimba mapiri, ndi nthambi zake zikunga mikungudza ya Mulungu. Unatambalitsa mphanda zake mpaka kunyanja, ndi mitsitsi yake kufikira ku Mtsinje. Munapasuliranji maphambo ake, kotero kuti onse akupita m'njira atcherako? Nguluwe zochokera kuthengo ziukumba, ndi nyama za kuchidikha ziudya. Bwererani, tikupemphani, Mulungu wa makamu; suzumirani muli m'mwamba, nimupenye, ndi kuzonda mpesa uwu, ndi tsinde limene dzanja lanu lamanja linaoka, ndi mphanda munadzilimbikitsira. Unapserera ndi moto, unadulidwa; aonongeka pa kudzudzula kwa nkhope yanu. Dzanja lanu likhale pa munthu wa pa dzanja lamanja lanu; pa mwana wa munthu amene munadzilimbikitsira. Potero sitidzabwerera m'mbuyo kukusiyani; titsitsimutseni, ndipo tidzaitanira dzina lanu. Mutibweze, Yehova Mulungu wa makamu; nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka. Kwa Mkulu wa Nyimbo, pa Gititi. Salimo la Asafu. Imbitsirani Mulungu ndiye mphamvu yathu; fuulirani kwa Mulungu wa Yakobo. Utsani salimo, bwera nakoni kalingaka, zeze wokondwetsa pamodzi ndi chisakasa. Ombani lipenga, pokhala mwezi, utakula mwezi, tsiku la phwando lathu. Pakuti ichi ndi cholemba cha kwa Israele, chiweruzo cha Mulungu wa Yakobo. Anachiika chikhale mboni kwa Yosefe, pakutuluka iye kudziko la Ejipito. Komwe ndinamva chinenedwe chosadziwa ine. Ndinamchotsera katundu paphewa pake, manja ake anamasuka ku chotengera. Unaitana posautsika, ndipo ndinakulanditsa; ndinakuvomereza mobisalika m'bingu; ndinakuyesa kumadzi a Meriba. Tamvani, anthu anga, ndidzakuchitirani mboni; Israele, ukadzandimvera! Kwanu kusakhale mulungu wofuma kwina; nusagwadire mulungu wachilendo. Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakukweza kukuchotsa kudziko la Ejipito; yasamitsa pakamwa pako ndipo ndidzalidzaza. Koma anthu anga sanamvere mau anga; ndipo Israele sanandivomere. Potero ndinawaperekera kuuma mtima kwao, ayende monga mwa uphungu waowao. Ha! Akadandimvera anthu anga, akadayenda m'njira zanga Israele! Ndikadagonjetsa adani ao msanga, ndikadabweza dzanja langa pa owasautsa. Akumuda Yehova akadamgonjera mungakhale monyenga, koma nyengo yao ikadakhala yosatha. Akadawadyetsa naye tirigu wokometsetsa, ndikadakukhutitsanso ndi uchi wa m'thanthwe. Salimo la Asafu. Mulungu aima mu msonkhano wa Mulungu, aweruza pakati pa milungu. Mudzaweruza mosalunjika kufikira liti, ndi kusamalira nkhope ya oipa? Weruzani osauka ndi amasiye; weruzani molungama ozunzika ndi osowa. Pulumutsani osauka ndi aumphawi; alanditseni m'dzanja la oipa. Sadziwa, ndipo sazindikira; amayendayenda mumdima; maziko onse a dziko lapansi agwedezeka. Ndinati Ine, Inu ndinu milungu, ndi ana a Wam'mwambamwamba nonsenu. Komatu mudzafa monga anthu, ndipo mudzagwa monga wina wa akulu. Ukani, Mulungu, weruzani dziko lapansi; pakuti Inu mudzalandira amitundu onse. Nyimbo. Salimo la Asafu. Mulungu musakhale chete; musakhale duu, osanena kanthu, Mulungu. Pakuti taonani, adani anu aphokosera, ndipo okwiyira Inu aweramutsa mutu. Apangana mochenjerera pa anthu anu, nakhalira upo pa obisika anu. Amati, Tiyeni tiwaononge asakhalenso mtundu wa anthu; ndipo dzina la Israele lisakumbukikenso. Pakuti anakhalira upo ndi mtima umodzi; anachita chipangano cha pa Inu. Mahema a Edomu ndi a Aismaele; Mowabu ndi Ahagiri; Gebala ndi Amoni ndi Amaleke; Filistiya, pamodzi ndi iwo okhala m'Tiro. Asiriya anaphatikana nao; anakhala dzanja la ana a Loti. Muwachitire monga munachitira Midiyani; ndi Sisera, ndi Yabini kumtsinje wa Kisoni, amene anaonongeka ku Endori; anakhala ngati ndowe ya kumunda. Muwaike akulu ao ngati Orebu ndi Zeebu; mafumu ao ngati Zeba ndi Zalimuna, amene anati, Tilande malo okhalamo Mulungu, akhale athu. Mulungu wanga, muwaike akhale ngati mungu; ngati ziputu zomka ndi mphepo. Monga moto upsereza nkhalango, ndi monga lawi liyatsa mapiri. Momwemo muwatsate ndi namondwe, nimuwaopse ndi kamvulumvulu wanu. Achititseni manyazi pankhope pao; kuti afune dzina lanu, Yehova. Achite manyazi, naopsedwe kosatha; ndipo asokonezeke, naonongeke. Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba pa dziko lonse lapansi. Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Gititi; Salimo la ana a Kora. Pokhala Inu mpotikonda ndithu, Yehova wa makamu! Moyo wanga ulakalaka, inde ukomokanso ndi kufuna mabwalo a Yehova; mtima wanga ndi thupi langa zifuulira kwa Mulungu wamoyo. Mbawanso inapeza nyumba, ndi namzeze chisa chake choikamo ana ake, pa maguwa a nsembe anu, Yehova wa makamu, mfumu yanga ndi Mulungu wanga. Odala iwo akugonera m'nyumba mwanu; akulemekezani chilemekezere. Wodala munthu amene mphamvu yake ili mwa Inu; mumtima mwake muli makwalala a ku Ziyoni. Popyola chigwa cha kulira misozi achiyesa cha akasupe; inde mvula ya chizimalupsa ichidzaza ndi madalitso. Apita mwamphamvu naonjezapo mphamvu, aoneka pamaso pa Mulungu m'Ziyoni. Yehova Mulungu wa makamu, imvani pemphero langa. Tcherani khutu, Mulungu wa Yakobo. Onani, Mulungu, ndinu chikopa chathu; ndipo penyani pa nkhope ya Wodzozedwa wanu. Pakuti tsiku limodzi m'mabwalo anu likoma koposa masiku ambirimbiri akukhala pena. Kukhala ine wapakhomo m'nyumba ya Mulungu wanga, kundikonda ine koposa kugonera m'mahema a choipa. Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa; Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero; sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro. Yehova wa makamu, wodala munthu wakukhulupirira Inu. Kwa Mkulu wa Nyimbo; Salimo la ana a Kora. Munachita zovomereza dziko lanu, Yehova; munabweza ukapolo wa Yakobo. Munachotsa mphulupulu ya anthu anu, munafotsera zolakwa zao zonse. Munabweza kuzaza kwanu konse; munabwerera kumkwiyo wanu wotentha. Mutibweze, Mulungu wa chipulumutso chathu, nimuletse udani wanu wa pa ife. Kodi mudzatikwiyira nthawi zonse? Kodi mudzakhala chikwiyire mibadwomibadwo? Kodi simudzatipatsanso moyo, kuti anthu anu akondwerere ndi Inu? Tionetseni chifundo chanu, Yehova, tipatseni chipulumutso chanu. Ndidzamva cholankhula Mulungu Yehova; pakuti adzalankhula zamtendere ndi anthu ake, ndi okondedwa ake; koma asabwererenso kuchita zopusa. Indedi chipulumutso chake chili pafupi ndi iwo akumuopa Iye; kuti m'dziko mwathu mukhale ulemu. Chifundo ndi choonadi zakomanizana; chilungamo ndi mtendere zapsompsonana. Choonadi chiphukira m'dziko; ndi chilungamo chasuzumira chili m'mwamba. Inde Yehova adzapereka zokoma; ndipo dziko lathu lidzapereka zipatso zake. Chilungamo chidzamtsogolera; nichidzamkonzera mapazi ake njira. Pemphero la Davide Tcherani khutu lanu Yehova, mundiyankhe; pakuti ine ndine wozunzika ndi waumphawi. Sungani moyo wanga pakuti ine ndine wokondedwa wanu; Inu Mulungu wanga, pulumutsani mtumiki wanu wokhulupirira Inu. Mundichitire chifundo, Ambuye; pakuti tsiku lonse ndiitana Inu. Kondwetsani moyo wa mtumiki wanu; pakuti ndikwezera moyo wanga kwa Inu, Ambuye. Pakuti Inu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira, ndi wa chifundo chochulukira onse akuitana Inu. Tcherani khutu pemphero langa, Yehova; nimumvere mau a kupemba kwanga. Tsiku la msauko wanga ndidzaitana Inu; popeza mudzandivomereza. Pakati pa milungu palibe wina wonga Inu, Ambuye; ndipo palibe ntchito zonga zanu. Amitundu onse mudawalenga adzadza nadzagwada pamaso panu, Ambuye; nadzalemekeza dzina lanu. Pakuti Inu ndinu wamkulu, ndi wakuchita zodabwitsa; Inu ndinu Mulungu, nokhanu. Mundionetse njira yanu, Yehova; ndidzayenda m'choonadi chanu, muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliope dzina lanu. Ndidzakuyamikani, Ambuye, Mulungu wanga, ndi mtima wanga wonse; ndipo ndidzalemekeza dzina lanu nthawi zonse. Pakuti chifundo chanu cha pa ine nchachikulu; ndipo munalanditsa moyo wanga kunsi kwa manda. Mulungu, odzikuza andiukira, ndi msonkhano wa anthu oopsa afuna moyo wanga, ndipo sanaike Inu pamaso pao. Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wansoni ndi wachisomo, wopatsa mtima msanga, ndi wochulukira chifundo ndi choonadi. Mundibwerere ine, ndi kundichitira chifundo; mpatseni mtumiki wanu mphamvu yanu, ndipo pulumutsani mwana wa mdzakazi wanu. Mundichitire chizindikiro choti chabwino; kuti ondida achione, nachite manyazi, popeza Inu, Yehova, munandithandiza ndi kundisangalatsa. Salimo la ana a Kora. Nyimbo. Maziko ake ali m'mapiri oyera. Yehova akonda zipata za Ziyoni koposa zokhalamo zonse za Yakobo. Mudzi wa Mulungu, inu, akunenerani zakukulemekezani. Ndidzatchula Rahabu ndi Babiloni kwa iwo ondidziwa Ine; taonani, Filistiya ndi Tiro pamodzi ndi Kusi; uyu anabadwa komweko. Ndipo adzanena za Ziyoni, uyu ndi uyo anabadwa m'mwemo; ndipo Wam'mwambamwamba ndiye adzaukhazikitsa. Yehova adzawerenga, polembera mitundu ya anthu, uyu anabadwa komweko. Ndipo oimba ndi oomba omwe adzati, akasupe anga onse ali mwa inu. Nyimbo, Salimo la ana a Kora. Kwa Mkulu wa Nyimbo, pa Mahalati Leanoti. Chilangizo cha Hemani Mwezara. Yehova, Mulungu wa chipulumutso changa, ndinafuula pamaso panu usana ndi usiku. Pemphero langa lidze pamaso panu; munditcherere khutu kukuwa kwanga. Pakuti mzimu wanga wadzala nao mavuto, ndi moyo wanga wayandikira kumanda. Anandiwerenga pamodzi nao otsikira kudzenje; ndakhala ngati munthu wopanda mphamvu. Wotayika pakati pa akufa, ngati ophedwa akugona m'manda, amene simuwakumbukiranso; ndipo anawadula kusiyana ndi dzanja lanu. Munandiika kunsi kwa dzenje, kuli mdima, kozama. Mkwiyo wanu utsamira pa ine, ndipo munandizunza ine ndi mafunde anu onse. Munandisiyanitsira wodziwana nane kutali; munandiika ndiwakhalire chonyansa. Ananditsekereza, osakhoza kutuluka ine. Diso langa lapuwala chifukwa cha kuzunzika kwanga: Ndimaitana Inu, Yehova, tsiku lonse; nditambalitsira manja anga kwa Inu. Kodi mudzachitira akufa zodabwitsa? Kodi adzaukanso otisiyawo, ndi kukulemekezani? Adzafotokozera chifundo chanu kumanda kodi, chikhulupiriko chanu kumalo a chionongeko? Zodabwitsa zanu zidadziwika mumdima kodi, ndi chilungamo chanu m'dziko la chiiwaliko? Koma ndinafuulira kwa Inu, Yehova, ndipo pemphero langa lifika kwa Inu mamawa. Yehova mutayiranji moyo wanga? Ndi kundibisira nkhope yanu? Wozunzika ine ndi wofuna kufa kuyambira ubwana wanga; posenza zoopsa zanu, ndithedwa nzeru. Kuzaza kwanu kwandimiza; zoopsa zanu zinandiononga. Zinandizungulira ngati madzi tsiku lonse; zinandizinga pamodzi. Munandichotsera kutali wondikonda ndi bwenzi langa, odziwana nane akhala kumdima. Chilangizo cha Etani Mwezara. Ndidzaimbira zachifundo za Yehova nthawi yonse, pakamwa panga ndidzadziwitsira chikhulupiriko chanu ku mibadwomibadwo. Pakuti ndinati, Chifundo adzachimanga kosaleka; mudzakhazika chikhulupiriko chanu m'Mwamba mwenimweni. Ndinachita chipangano ndi wosankhika wanga, ndinalumbirira Davide mtumiki wanga. Ndidzakhazika mbeu yako kunthawi yonse, ndipo ndidzamanga mpando wachifumu wako ku mibadwomibadwo. Ndipo kumwamba kudzalemekeza zodabwitsa zanu, Yehova; chikhulupiriko chanunso mu msonkhano wa oyera mtima. Pakuti kuli yani kuthambo timlinganize ndi Yehova? Afanana ndi Yehova ndani mwa ana a amphamvu? Ndiye Mulungu, ayenera kumuopa kwambiri m'upo wa oyera mtima, ndiye wochititsa mantha koposa onse akumzinga. Yehova, Mulungu wa makamu, wamphamvu ndani wonga Inu, Yehova? Ndipo chikhulupiriko chanu chikuzingani. Inu ndinu wakuchita ufumu pa kudzikuza kwa nyanja; pakuuka mafunde ake muwachititsa bata. Mudathyola Rahabu, monga munthu wophedwa; munabalalitsa adani anu ndi mkono wa mphamvu yanu. Kumwamba ndi kwanu, dziko lapansi lomwe ndi lanu; munakhazika dziko lokhalamo anthu ndi kudzala kwake. Munalenga kumpoto ndi kumwera; Tabori ndi Heremoni afuula mokondwera m'dzina lanu. Muli nao mkono wanu wolimba; m'dzanja mwanu muli mphamvu, dzanja lamanja lanu nlokwezeka. Chilungamo ndi chiweruzo ndiwo maziko a mpando wachifumu wanu; chifundo ndi choonadi zitsogolera pankhope panu. Odala anthu odziwa liu la lipenga; ayenda m'kuunika kwa nkhope yanu, Yehova. Akondwera m'dzina lanu tsiku lonse; ndipo akwezeka m'chilungamo chanu. Popeza Inu ndinu ulemerero wa mphamvu yao; ndipo potivomereza Inu nyanga yathu idzakwezeka. Pakuti chikopa chathu chifuma kwa Yehova; ndi mfumu yathu kwa Woyera wa Israele. Pamenepo munalankhula m'masomphenya ndi okondedwa anu, ndipo mudati, Ndasenza thandizo pa chiphona; ndakweza wina wosankhika mwa anthu. Ndapeza Davide mtumiki wanga; ndamdzoza mafuta anga oyera. Amene dzanja langa lidzakhazikika naye; inde mkono wanga udzalimbitsa. Mdani sadzamuumira mtima; ndi mwana wa chisalungamo sadzamzunza. Ndipo ndidzaphwanya omsautsa pamaso pake; ndidzapandanso odana naye. Koma chikhulupiriko changa ndi chifundo changa zidzakhala naye; ndipo nyanga yake idzakwezeka m'dzina langa. Ndipo ndidzaika dzanja lake panyanja, ndi dzanja lamanja lake pamitsinje. Iye adzanditchula, ndi kuti, Inu ndinu Atate wanga, Mulungu wanga, ndi thanthwe la chipulumutso changa. Inde ndidzamuyesa mwana wanga woyamba, womveka wa mafumu a pa dziko lapansi. Ndidzamsungira chifundo changa kunthawi yonse, ndipo chipangano changa chidzalimbika pa iye. Ndidzakhalitsanso mbeu yake chikhalire, ndi mpando wachifumu wake ngati masiku a m'mwamba. Ana ake akataya chilamulo changa, osayenda m'maweruzo anga, nakaipsa malembo anga; osasunga malamulo anga. Pamenepo ndidzazonda zolakwa zao ndi ndodo, ndi mphulupulu zao ndi mikwingwirima. Koma sindidzamchotsera chifundo changa chonse, ndi chikhulupiriko changa sichidzamsowa. Sindidzaipsa chipangano changa, kapena kusintha mau otuluka m'milomo yanga. Ndinalumbira kamodzi m'chiyero changa; sindidzanamizira Davide. Mbeu yake idzakhala kunthawi yonse, ndi mpando wachifumu wake ngati dzuwa pamaso panga. Udzakhazikika ngati mwezi kunthawi yonse, ndi ngati mboni yokhulupirika kuthambo. Koma Inu munamtaya, nimunamkaniza, munakwiya naye wodzozedwa wanu. Munakaniza chipangano cha mtumiki wanu; munaipsa korona wake ndi kumponya pansi. Munapasula makoma ake onse; munagumula malinga ake. Onse opita panjirapa amfunkhira, akhala chotonza cha anansi ake. Munakweza dzanja lamanja la iwo omsautsa; munakondweretsa adani ake onse. Munapinditsa kukamwa kwake kwa lupanga lake, osamuimika kunkhondo. Munaleketsa kuwala kwake, ndipo munagwetsa pansi mpando wachifumu wake. Munafupikitsa masiku a mnyamata wake; munamkuta nao manyazi. Mudzabisala kosatha kufikira liti, Yehova; ndi kuzaza kwanu kudzatentha ngati moto kufikira liti? Kumbukirani kuti nthawi yanga njapafupi; munalengeranji ana onse a anthu kwachabe? Munthu ndani amene adzakhalabe ndi moyo, osaona imfa? Amene adzapulumutsa moyo wake kumphamvu ya manda? Chilikuti chifundo chanu chakale, Ambuye, munachilumbirira Davide pa chikhulupiriko chanu? Kumbukirani, Ambuye, chotonzera atumiki anu; ndichisenza m'chifuwa mwanga chochokera kumitundu yonse yaikulu ya anthu. Chimene adani anu, Yehova, atonza nacho; chimene atonzera nacho mayendedwe a wodzozedwa wanu. Wodalitsika Yehova kunthawi yonse. Amen ndi Amen. Pemphero la Mose munthu wa Mulungu. Ambuye, Inu munatikhalira mokhalamo m'mibadwomibadwo. Asanabadwe mapiri, kapena musanalenge dziko lapansi, ndi lokhalamo anthu, inde, kuyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha, Inu ndinu Mulungu. Mubweza munthu akhale fumbi; nimuti, Bwererani inu, ana a anthu. Pakuti pamaso panu zaka zikwi zikhala ngati dzulo, litapita, ndi monga ulonda wa usiku. Muwatenga ngati ndi madzi aakulu, akhala ngati tulo; mamawa akhala ngati msipu wophuka. Mamawa uphuka bwino; madzulo ausenga, nuuma. Pakuti tionongeka mu mkwiyo wanu; ndipo m'kuzaza kwanu tiopsedwa. Munaika mphulupulu zathu pamaso panu, ndi zoipa zathu zobisika pounikira nkhope yanu. Pakuti masiku athu onse apitirira m'ukali wanu; titsiriza moyo wathu ngati lingaliro. Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu ndi awiri, kapena tikakhala nayo mphamvudi zaka makumi asanu ndi atatu; koma teronso kukula kwao kumati chivuto ndi chopanda pake; pakuti kumapitako msanga ndipo tithawa ife tomwe. Adziwa mphamvu ya mkwiyo wanu ndani, ndi ukali wanu monga ayenera kukuopani? Mutidziwitse kuwerenga masiku athu motero, kuti tikhale nao mtima wanzeru. Bwerani, Yehova; kufikira liti? Ndipo alekeni atumiki anu. Mutikhutitse nacho chifundo chanu m'mawa; ndipo tidzafuula mokondwera ndi kukondwera masiku athu onse. Tikondweretseni monga mwa masiku mudatizunzawa, ndi zaka tidaona choipa. Chochita Inu chioneke kwa atumiki anu, ndi ulemerero wanu pa ana ao. Ndipo chisomo chake cha Yehova Mulungu wathu chikhalire pa ife; ndipo mutikhazikitsire ife ntchito ya manja athu; inde, ntchito ya manja athu muikhazikitse. Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse. Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira. Pakuti adzakuonjola kumsampha wa msodzi, kumliri wosakaza. Adzakufungatira ndi nthenga zake, ndipo udzathawira kunsi kwa mapiko ake; choonadi chake ndicho chikopa chotchinjiriza. Sudzaopa choopsa cha usiku, kapena muvi wopita usana; kapena mliri woyenda mumdima, kapena chionongeko chakuthera usana. Pambali pako padzagwa chikwi, ndi zikwi khumi pa dzanja lamanja lako; sichidzakuyandikiza iwe. Koma udzapenya ndi maso ako, nudzaona kubwezera chilango oipa. Popeza udati, Inu Yehova, ndinu pothawirapo panga! Udaika Wam'mwambamwamba chokhalamo chako; palibe choipa chidzakugwera, ndipo cholanga sichidzayandikiza hema wako. Pakuti adzalamulira angelo ake za iwe, akusunge m'njira zako zonse. Adzakunyamula pa manja ao, ungagunde phazi lako pamwala. Udzaponda mkango ndi mphiri; udzapondereza msona wa mkango ndi chinjoka. Popeza andikondadi ndidzampulumutsa; ndidzamkweza m'mwamba, popeza adziwa dzina langa. Adzandifuulira Ine ndipo ndidzamyankha; kunsautso ndidzakhala naye pamodzi; ndidzamlanditsa, ndi kumchitira ulemu. Ndidzamkhutitsa ndi masiku ambiri, ndi kumuonetsera chipulumutso changa. Salimo, Nyimbo ya pa Sabata. Nkokoma kuyamika Yehova, ndi kuimbira nyimbo dzina lanu, Wam'mwambamwamba Inu. Kuonetsera chifundo chanu mamawa, ndi chikhulupiriko chanu usiku uliwonse. Pa choimbira cha zingwe khumi ndi pachisakasa; pazeze ndi kulira kwake. Popeza Inu, Yehova, munandikondweretsa ndi kuchita kwanu, ndidzafuula mokondwera pa ntchito ya manja anu. Ha! Ntchito zanu nzazikulu, Yehova, zolingalira zanu nzozama ndithu. Munthu wopulukira sachidziwa; ndi munthu wopusa sachizindikira ichi; chakuti pophuka oipa ngati msipu, ndi popindula ochita zopanda pake; chitero kuti adzaonongeke kosatha. Koma Inu, Yehova, muli m'mwamba kunthawi yonse. Pakuti, taonani, adani anu, Yehova, pakuti, taonani, adani anu adzatayika; ochita zopanda pake onse adzamwazika. Koma munakweza nyanga yanga ngati ya njati; anandidzoza mafuta atsopano. Diso langa lapenya chokhumba ine pa iwo ondilalira, m'makutu mwanga ndamva chokhumba ine pa iwo akuchita zoipa akundiukira. Wolungama adzaphuka ngati mgwalangwa; adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni. Iwo ookedwa m'nyumba ya Yehova, adzaphuka m'mabwalo a Mulungu wathu. Atakalamba adzapatsanso zipatso; adzadzazidwa ndi madzi nadzakhala abiriwiri, kulalikira kuti Yehova ngwolunjika; Iye ndiye thanthwe langa, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama. Yehova achita ufumu; wadziveka ndi ukulu; wadziveka Yehova, wadzimangirira mphamvu m'chuuno; dziko lomwe lokhalamo anthu likhakizika, silidzagwedezeka. Mpando wachifumu wanu ukhazikika kuyambira kale lija; Inu ndinu wosayambira ndi kale lomwe. Mitsinje ikweza, Yehova, mitsinje ikweza mkokomo wao; mitsinje ikweza mafunde ao. Yehova Wam'mwamba ndiye wamphamvu, wakuposa mkokomo wa madzi ambiri, ndi mafunde olimba a nyanja. Mboni zanu zivomerezeka ndithu; chiyero chiyenera nyumba yanu, Yehova, kunthawi za muyaya. Mulungu wakubwezera chilango, Yehova, Mulungu wakubwezera chilango, muoneke wowala. Nyamukani, Inu woweruza wa dziko lapansi: Bwezerani odzikuza choyenera iwo. Oipa adzatumpha ndi chimwemwe kufikira liti, Yehova? Oipa adzatero kufikira liti? Anena mau, alankhula zowawa; adzitamandira onse ochita zopanda pake. Aphwanya anthu anu, Yehova, nazunza cholandira chanu. Amapha wamasiye ndi mlendo, nawapha ana amasiye. Ndipo amati, Yehova sachipenya, ndi Mulungu wa Yakobo sachisamalira. Zindikirani, opulukira inu mwa anthu; ndipo opusa inu, mudzachita mwanzeru liti? Kodi Iye wakupanga khutu ngwosamva? Kodi Iye wakuumba diso ngwosapenya? Kodi Iye wakulangiza mitundu ya anthu, ndiye wosadzudzula? Si ndiye amene aphunzitsa munthu nzeru? Yehova adziwa zolingalira za munthu, kuti zili zachabe. Wodala munthu amene mumlanga, Yehova; ndi kumphunzitsa m'chilamulo chanu; kuti mumpumitse masiku oipa; kufikira atakumbira woipa mbuna. Pakuti Yehova sadzasiya anthu ake, ndipo sadzataya cholandira chake. Pakuti chiweruzo chidzabwera kunka kuchilungamo, ndipo oongoka mtima onse adzachitsata. Adzandiukira ndani kutsutsana nao ochita zoipa? Adzandilimbikira ndani kutsutsana nao ochita zopanda pake? Akadapanda kukhala thandizo langa Yehova, moyo wanga ukadakhala kuli chete. Pamene ndinati, Litereka phazi langa, chifundo chanu, Yehova, chinandichirikiza. Pondichulukira zolingalira zanga m'kati mwanga, zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga. Kodi uyenera kuyanjana ndi Inu mpando wachifumu wa kusakaza, wakupanga chovuta chikhale lamulo? Asonkhana pamodzi pa moyo wa wolungama, namtsutsa wa mwazi wosachimwa. Koma Yehova wakhala msanje wanga; ndi Mulungu wanga thanthwe lothawirapo ine. Ndipo anawabwezera zopanda pake zao, nadzawaononga m'choipa chao; Yehova Mulungu wathu adzawaononga. Tiyeni tiimbire Yehova mokondwera; tifuule kwa thanthwe la chipulumutso chathu. Tidze nacho chiyamiko pamaso pake, timfuulire Iye mokondwera ndi nyimbo. Pakuti Yehova ndiye Mulungu wamkulu; ndi mfumu yaikulu yoposa milungu yonse. Malo ozama a dziko lapansi ali m'dzanja lake; chuma cha m'mapiri chomwe ndi chake. Nyanja ndi yake, anailenga; ndipo manja ake anaumba dziko louma. Tiyeni, tipembedze tiwerame; tigwade pamaso pa Yehova, amene anatilenga. Pakuti Iye ndiye Mulungu wathu, ndipo ife ndife anthu a pabusa pake, ndi nkhosa za m'dzanja mwake. Lero, mukamva mau ake! Musaumitse mitima yanu, ngati ku Meriba, ngati tsiku la ku Masa m'chipululu. Pamene makolo anu anandisuntha, anandiyesa, anapenyanso chochita Ine. Zaka makumi anai mbadwo uwu unandimvetsa chisoni, ndipo ndinati, Iwo ndiwo anthu osokerera mtima, ndipo sadziwa njira zanga. Chifukwa chake ndinalumbira mu mkwiyo wanga, ngati adzalowa mpumulo wanga. Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano; muimbireni Yehova, inu, dziko lonse lapansi. Muimbireni Yehova, lemekezani dzina lake; lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku. Fotokozerani ulemerero wake mwa amitundu; zodabwitsa zake mwa mitundu yonse ya anthu. Pakuti Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ayenera amuope koposa milungu yonse. Pakuti milungu yonse ya mitundu ya anthu ndiyo mafano, koma Yehova analenga zakumwamba. Pamaso pake pali ulemu ndi ukulu. M'malo opatulika mwake muli mphamvu ndi zochititsa kaso. Mpatseni Yehova, inu, mafuko a mitundu ya anthu, mpatseni Yehova ulemerero ndi mphamvu. Mpatseni Yehova ulemerero wa dzina lake; bwerani nacho chopereka, ndipo fikani kumabwalo ake. Gwadirani Yehova moyera ndi mokometsetsa, njenjemerani pamaso pake, inu dziko lonse lapansi. Nenani mwa amitundu, Yehova achita ufumu; dziko lokhalamo anthu lomwe likhazikika kuti silingagwedezeke; adzaweruza mitundu ya anthu molunjika. Kumwamba kukondwere nilisekerere dziko lapansi; nyanja ibume mwa kudzala kwake. Munda ukondwerere ndi zonse zili m'mwemo; pamenepo mitengo yonse ya kunkhalango idzafuula mokondwera. Pamaso pa Yehova, pakuti akudza; pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi Adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo, ndi mitundu ya anthu ndi choonadi. Yehova achita ufumu; dziko lapansi likondwere; zisumbu zambiri zikondwerere. Pomzinga pali mitambo ndi mdima; chilungamo ndi chiweruzo ndizo zolimbitsa mpando wachifumu wake. Moto umtsogolera, nupsereza otsutsana naye pozungulirapo. Mphezi zake zinaunikira dziko lokhalamo anthu; dziko lapansi linaona nilinagwedezeka. Mapiri anasungunuka ngati sera pamaso pa Yehova, pamaso pa Ambuye wa dziko lonse lapansi. Kumwamba kulalikira chilungamo chake, ndipo mitundu yonse ya anthu ipenya ulemerero wake. Onse akutumikira fano losema, akudzitamandira nao mafano, achite manyazi: Mgwadireni Iye, milungu yonse inu. Ziyoni anamva nakondwera, nasekerera ana akazi a Yuda; chifukwa cha maweruzo anu, Yehova. Pakuti Inu, Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba pa dziko lonse lapansi, ndinu wokwezeka kwakukulu pamwamba pa milungu yonse ina. Inu okonda Yehova, danani nacho choipa: Iye asunga moyo wa okondedwa ake; awalanditsa m'manja mwa oipa. Kuunika kufesekera wolungama, ndi chikondwerero oongoka mtima. Kondwerani mwa Yehova, olungama inu; ndipo yamikani pokumbukira chiyero chake. Salimo. Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano; popeza anachita zodabwitsa: Dzanja lake lamanja, mkono wake woyera, zinamchitira chipulumutso. Yehova anawadziwitsira chipulumutso chake; anaonetsera chilungamo chake pamaso pa amitundu. Anakumbukira chifundo chake ndi chikhulupiriko chake kunyumba ya Israele; malekezero onse a dziko lapansi anaona chipulumutso cha Mulungu wathu. Fuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi; kuwitsani ndi kufuulira mokondwera; inde, imbirani zomlemekeza. Muimbireni Yehova zomlemekeza ndi zeze; ndi zeze ndi mau a salimo. Fuulani pamaso pa Mfumu Yehova, ndi mbetete ndi liu la lipenga. Nyanja ifuule ndi kudzala kwake; dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhalamo; mitsinje iombe manja; mapiri afuule pamodzi mokondwera. Pamaso pa Yehova, popeza akudza kudzaweruza dziko lapansi; adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo, ndipo mitundu ya anthu molunjika. Yehova ndiye mfumu; mitundu ya anthu injenjemere; Iye akhala pakati pa akerubi; dziko lapansi ligwedezeke. Yehova ndiye wamkulu m'Ziyoni; ndipo akwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu. Alemekeze dzina lanu lalikulu ndi loopsa. Ili ndilo loyera. Ndipo mphamvu ya mfumu ikonda chiweruzo; Inu mukhazikitsa zolunjika, muchita chiweruzo ndi chilungamo m'Yakobo. Mkwezeni Yehova Mulungu wathu, ndipo gwadirani poponderapo mapazi ake: Iye ndiye Woyera. Mwa ansembe ake muli Mose ndi Aroni, ndi Samuele mwa iwo akuitanira dzina lake; anaitana kwa Yehova, ndipo Iye anawayankha. Iye analankhula nao mu mtambo woti njo: Iwo anasunga mboni zake ndi malembawa anawapatsa. Munawayankha, Yehova Mulungu wathu: munawakhalira Mulungu wakuwakhululukira, mungakhale munabwezera chilango pa zochita zao. Mkwezeni Yehova Mulungu wathu, ndipo gwadirani pa phiri lake loyera; pakuti Yehova Mulungu wathu ndiye woyera. Salimo la Chiyamiko. Fuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi. Tumikirani Yehova ndi chikondwerero: Idzani pamaso pake ndi kumuimbira mokondwera. Dziwani kuti Yehova ndiye Mulungu; Iyeyu anatilenga, ndipo ife ndife ake; ndife anthu ake ndi nkhosa zapabusa pake. Lowani kuzipata zake ndi chiyamiko, ndi kumabwalo ake ndi chilemekezo: Myamikeni; lilemekezeni dzina lake. Pakuti Yehova ndiye wabwino; chifundo chake chimanka muyaya; ndi chikhulupiriko chake ku mibadwomibadwo. Salimo la Davide. Ndidzaimba zachifundo ndi chiweruzo; ndidzaimba zakukulemekezani Inu, Yehova. Ndidzachita mwanzeru m'njira yangwiro; mudzandidzera liti? Ndidzayenda m'nyumba mwanu ndi mtima wangwiro. Sindidzaika chinthu choipa pamaso panga; chochita iwo akupatuka padera chindiipira; sichidzandimamatira. Mtima wopulukira udzandichokera; sindidzadziwana naye woipa. Wakuneneza mnzake m'tseri ndidzamdula; wa maso odzikuza ndi mtima wodzitama sindidzamlola. Maso anga ayang'ana okhulupirika m'dziko, kuti akhale ndi Ine; iye amene ayenda m'njira yangwiro, iyeyu adzanditumikira Ine. Wakuchita chinyengo sadzakhala m'kati mwa nyumba yanga; wakunena mabodza sadzakhazikika pamaso panga. Mamawa onse ndidzadula oipa onse a m'dziko; kuduliratu onse akuchita zopanda pake kumudzi wa Yehova. Pemphero la Wozunzika, m'mene anakomoka natsanulira cholingalira chake pamaso pa Yehova. Yehova, imvani pemphero langa, ndipo mfuu wanga ufikire Inu. Musandibisire nkhope yanu tsiku la nsautso yanga; munditchereze khutu lanu; tsiku limene ndiitana ine mundiyankhe msanga. Popeza masiku anga akanganuka ngati utsi, ndi mafupa anga anyeka ngati nkhuni. Mtima wanga ukunga udzu womweta, nufota; popeza ndiiwala kudya mkate wanga. Chifukwa cha liu la kubuula kwanga mnofu wanga umamatika kumafupa anga. Ndikunga vuwo m'chipululu; ndikhala ngati kadzidzi wa kumabwinja. Ndidikira, ndikhala ngati mbalame ili yokha pamwamba pa tsindwi. Adani anga anditonza tsiku lonse; akundiyalukirawo alumbirira ine. Pakuti ndadya mapulusa ngati mkate, ndi kusanganiza chomwera changa ndi misozi, chifukwa cha ukali wanu ndi kuzaza kwanu; popeza munandinyamula ndipo munandigwetsa. Masiku anga akunga mthunzi womka m'tali; ndipo ine ndauma ngati udzu. Koma Inu, Yehova, mukhalabe kunthawi yonse; ndi chikumbukiro chanu ku mibadwomibadwo. Inu mudzauka, ndi kuchitira nsoni Ziyoni; popeza yafika nyengo yakumchitira chifundo, nyengo yoikika. Pakuti atumiki anu akondwera nayo miyala yake, nachitira chifundo fumbi lake. Pamenepo amitundu adzaopa dzina la Yehova, ndi mafumu onse a dziko lapansi ulemerero wanu. Pakuti Yehova anamanga Ziyoni, anaoneka m'ulemerero wake; anasamalira pemphero la iwo akusowa konse, osapepula pemphero lao. Ichi adzachilembera mbadwo ukudza; ndi mtundu wa anthu umene udalengedwa udzamlemekeza Yehova. Pakuti anapenya pansi ali kumwamba kuli malo ake opatulika; Yehova pokhala kumwamba anapenya dziko lapansi; kuti amve kubuula kwa wandende; namasule ana a imfa. Kuti anthu alalikire dzina la Yehova m'Ziyoni, ndi chilemekezo chake m'Yerusalemu; Posonkhana pamodzi mitundu ya anthu, ndi maufumu kuti atumikire Yehova. Iye analanda mphamvu yanga panjira; anachepsa masiku anga. Ndinati, Mulungu wanga, musandichotse pakati pa masiku anga: Zaka zanu zikhalira m'mibadwomibadwo. Munakhazika dziko lapansi kalelo; ndipo zakumwamba ndizo ntchito ya manja anu. Zidzatha izi, koma Inu mukhala: Inde, zidzatha zonse ngati chovala; mudzazisintha ngati malaya, ndipo zidzasinthika: Koma Inu ndinu yemweyo, ndi zaka zanu sizifikira kutha. Ana a atumiki anu adzakhalitsa, ndi mbeu zao zidzakhazikika pamaso panu. Salimo la Davide. Lemekeza Yehova, moyo wanga; ndi zonse za m'kati mwanga zilemekeze dzina lake loyera. Lemekeza Yehova, moyo wanga, ndi kusaiwala zokoma zake zonse atichitirazi: Amene akhululukira mphulupulu zako zonse; nachiritsa nthenda zako zonse; amene aombola moyo wako ungaonongeke; nakuveka korona wa chifundo ndi nsoni zokoma: Amene akhutitsa m'kamwa mwako ndi zabwino; nabweza ubwana wako unge mphungu. Yehova achitira onse osautsidwa chilungamo ndi chiweruzo. Analangiza Mose njira zake, ndi ana a Israele machitidwe ake. Yehova ndiye wa nsoni zokoma ndi wachisomo, wosakwiya msanga, ndi wa chifundo chochuluka. Sadzatsutsana nao nthawi zonse; ndipo sadzasunga mkwiyo wake kosatha. Sanatichitira monga mwa zolakwa zathu, kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu. Pakuti monga m'mwamba mutalikira ndi dziko lapansi, motero chifundo chake chikulira iwo akumuopa Iye. Monga kum'mawa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu. Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye. Popeza adziwa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi. Koma munthu, masiku ake akunga udzu; aphuka monga duwa la kuthengo. Pakuti mphepo ikapitapo pakhala palibe: Ndi malo ake salidziwanso. Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana; kwa iwo akusunga chipangano chake, ndi kwa iwo akukumbukira malangizo ake kuwachita. Yehova anakhazika mpando wachifumu wake Kumwamba; ndi ufumu wake uchita mphamvu ponsepo. Lemekezani Yehova, inu angelo ake; a mphamvu zolimba, akuchita mau ake, akumvera liu la mau ake. Lemekezani Yehova, inu makamu ake onse; inu atumiki ake akuchita chomkondweretsa Iye. Lemekezani Yehova, inu, ntchito zake zonse, ponseponse pali ufumu wake: Lemekeza Yehova, moyo wanga iwe. Lemekeza Yehova, moyo wanga; Yehova, Mulungu wanga, Inu ndinu wamkulukulu; muvala ulemu ndi chifumu. Amene mudzikuta nako kuunika monga ndi chovala; ndi kuyala thambo ngati nsalu yotchinga. Amene alumikiza mitanda ya zipinda zake m'madzi; naika makongwa akhale agaleta ake; nayenda pa mapiko a mphepo. Amene ayesa mphepo amithenga ake; lawi la moto atumiki ake; anakhazika dziko lapansi pa maziko ake, silidzagwedezeka kunthawi yonse. Mudalikuta ndi nyanja ngati ndi chovala; madzi anafikira pamwamba pa mapiri. Pa kudzudzula kwanu anathawa; anathawa msanga liu la bingu lanu; anakwera m'mapiri, anatsikira m'zigwa, kufikira malo mudawakonzeratu. Munaika malire kuti asapitirireko; kuti asabwererenso kuphimba dziko lapansi. Atumiza akasupe alowe m'makwawa; ayenda pakati pa mapiri: Zimamwamo nyama zonse za kuthengo; mbidzi zipherako ludzu lao. Mbalame za mlengalenga zifatsa pamenepo, zimaimba pakati pa mitawi. Iye amwetsa mapiri mochokera m'zipinda zake: Dziko lakhuta zipatso za ntchito zanu. Ameretsa msipu ziudye ng'ombe, ndi zitsamba achite nazo munthu; natulutse chakudya chochokera m'nthaka; ndi vinyo wokondweretsa mtima wa munthu, ndi mafuta akunyezimiritsa nkhope yake, ndi mkate wakulimbitsa mtima wa munthu. Mitengo ya Yehova yadzala ndi madzi; mikungudza ya ku Lebanoni imene anaioka; m'mwemo mbalame zimanga zisa zao; pokhala chumba mpa mitengo ya mikungudza. Mapiri atali ndiwo ayenera zinkhoma; pamatanthwe mpothawirapo mbira. Anaika mwezi nyengo zake; dzuwa lidziwa polowera pake. Muika mdima ndipo pali usiku; pamenepo zituluka zilombo zonse za m'thengo. Misona ya mkango ibangula potsata nyama yao, nifuna chakudya chao kwa Mulungu. Potuluka dzuwa, zithawa, zigona pansi m'ngaka mwao. Pamenepo munthu atulukira kuntchito yake, nagwiritsa kufikira madzulo. Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu. Nyanja siyo, yaikulu ndi yachitando, m'mwemo muli zokwawa zosawerengeka; zamoyo zazing'ono ndi zazikulu. M'mwemo muyenda zombo; ndi Leviyatani amene munamlenga aseweremo. Izi zonse zikulindirirani, muzipatse chakudya chao pa nyengo yake. Chimene muzipatsa zigwira; mufumbatula dzanja lanu, zikhuta zabwino. Mukabisa nkhope yanu, ziopsedwa; mukalanda mpweya wao, zikufa, nizibwerera kufumbi kwao. Potumizira mzimu wanu, zilengedwa; ndipo mukonzanso nkhope ya dziko lapansi. Ulemerero wa Yehova ukhale kosatha; Yehova akondwere mu ntchito zake; amene apenyerera pa dziko lapansi, ndipo linjenjemera; akhudza mapiri, ndipo afuka. Ndidzaimbira Yehova m'moyo mwanga: ndidzaimbira Mulungu wanga zomlemekeza pokhala ndilipo. Pomlingirira Iye pandikonde; ndidzakondwera mwa Yehova. Ochimwa athedwe kudziko lapansi, ndi oipa asakhalenso. Yamika Yehova, moyo wanga. Aleluya. Yamikani Yehova, itanirani pa dzina lake; bukitsani mwa mitundu ya anthu zochita Iye. Muimbireni, muimbireni zomlemekeza; fotokozerani zodabwitsa zake zonse. Mudzitamandire ndi dzina lake loyera: mitima yao ya iwo ofunsira Yehova ikondwere. Funani Yehova, ndi mphamvu yake; funsirani nkhope yake nthawi zonse. Kumbukirani zodabwitsa zake adazichita; zizindikiro zake ndi maweruzo a pakamwa pake; inu mbeu za Abrahamu, mtumiki wake, inu ana a Yakobo, osankhika ake. Iye ndiye Yehova, Mulungu wathu; maweruzo ake akhala pa dziko lonse lapansi. Akumbukira chipangano chake kosatha, mauwo anawalamulira mibadwo zikwi; chipanganocho anapangana ndi Abrahamu, ndi lumbiro lake ndi Isaki; ndipo anachiimikira Yakobo, chikhale malemba, chikhale chipangano chosatha kwa Israele. Ndi kunena kuti, Ndidzakupatsa iwe dziko la Kanani, gawo la cholandira chako; pokhala iwo anthu owerengeka, inde, anthu pang'ono, ndi alendo m'mwemo; nayendayenda kuchokera mtundu wina kufikira mtundu wina, kuchokera ufumu wina kufikira anthu ena. Sanalola munthu awasautse; ndipo anadzudzula mafumu chifukwa cha iwowa. Ndi kuti, Musamakhudza odzozedwa anga, musamachitira choipa aneneri anga. Ndipo anaitana njala igwere dziko; anathyola mchirikizo wonse wa mkate. Anawatsogozeratu munthu; anamgulitsa Yosefe akhale kapolo: Anapweteka miyendo yake ndi matangadza; anamgoneka m'unyolo; kufikira nyengo yakuchitika maneno ake; mau a Yehova anamuyesa. Mfumuyo anatuma munthu nammasula; woweruza mitundu ya anthu anamtsegulira. Anamuika akhale woyang'anira nyumba yake, ndi woweruza wa pa zake zonse: Amange nduna zake iye mwini, alangize akulu ake adziwe nzeru. Pamenepo Israele analowa m'Ejipito; ndi Yakobo anakhala mlendo m'dziko la Hamu. Ndipo anachulukitsatu mtundu wa anthu ake, nawapatsa mphamvu yoposa owasautsa. Anasanduliza mitima yao, kuti adane nao anthu ake, kuti achite monyenga ndi atumiki ake. Anatuma Mose mtumiki wake, ndi Aroni amene adamsankha. Anaika pakati pao zizindikiro zake, ndi zodabwitsa m'dziko la Hamu. Anatumiza mdima ndipo kunada; ndipo sanapikisane nao mau ake. Anasanduliza madzi ao akhale mwazi, naphanso nsomba zao. Dziko lao linachuluka achule, m'zipinda zomwe za mafumu ao. Ananena, ndipo inadza mitambo ya ntchentche, ndi nsabwe kufikira m'malire ao onse. Anawapatsa mvula yamatalala, lawi la moto m'dziko lao. Ndipo anapanda mipesa yao, ndi mikuyu yao; nathyola mitengo kufikira m'malire ao onse. Ananena, ndipo linadza dzombe ndi mphuchi, ndizo zosawerengeka, ndipo zinadya zitsamba zonse za m'dziko mwao, zinadyanso zipatso za m'nthaka mwao. Ndipo Iye anapha achisamba onse m'dziko mwao, choyambira cha mphamvu yao yonse. Ndipo anawatulutsa pamodzi ndi siliva ndi golide: ndi mwa mafuko ao munalibe mmodzi wokhumudwa. Ejipito anakondwera pakuchoka iwo; popeza kuopsa kwao kudawagwera. Anayala mtambo uwaphimbe; ndi moto uunikire usiku. Anafunsa ndipo Iye anadzetsa zinziri, nawakhutitsa mkate wakumwamba. Anatsegula pathanthwe, anatulukamo madzi; nayenda pouma ngati mtsinje. Popeza anakumbukira mau ake oyera, ndi Abrahamu mtumiki wake. Potero anatulutsa anthu ake ndi kusekerera, osankhika ake ndi kufuula mokondwera. Ndipo anawapatsa maiko a amitundu; iwo ndipo analanda zipatso za ntchito ya anthu: Kuti asamalire malemba ake, nasunge malamulo ake. Aleluya. Aleluya. Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino: Pakuti chifundo chake nchosatha. Adzafotokoza ndani ntchito zamphamvu za Yehova, adzamveketsa ndani chilemekezo chake chonse? Odala iwo amene asunga chiweruzo, iye amene achita chilungamo nthawi zonse. Mundikumbukire, Yehova, monga momwe muvomerezana ndi anthu anu; mundionetsa chipulumutso chanu: Kuti ndione chokomacho cha osankhika anu, kuti ndikondwere nacho chikondwerero cha anthu anu, kuti ndidzitamandire pamodzi ndi cholowa chanu. Talakwa pamodzi ndi makolo athu; tachita mphulupulu, tachita choipa. Makolo athu sanadziwitse zodabwitsa zanu m'Ejipito; sanakumbukire zachifundo zanu zaunyinji; koma anapikisana ndi Inu kunyanja, ku Nyanja Yofiira. Koma anawapulumutsa chifukwa cha dzina lake, kuti adziwitse chimphamvu chake. Ndipo anadzudzula Nyanja Yofiira, niiphwa: Potero anawayendetsa mozama ngati m'chipululu. Ndipo anawapulumutsa m'dzanja la iye amene anawada, nawaombola kudzanja la mdani. Ndipo madziwo anamiza owasautsa; sanatsale mmodzi yense. Pamenepo anavomereza mau ake; anaimbira chomlemekeza. Koma anaiwala ntchito zake msanga; sanalindire uphungu wake: Popeza analakalakatu kuchidikhako, nayesa Mulungu m'chipululu. Ndipo anawapatsa chopempha iwo; koma anaondetsa mitima yao. Ndipo kumisasa anachita nao nsanje Mose ndi Aroni woyerayo wa Yehova. Dziko lidayasama nilidameza Datani, ndipo linafotsera gulu la Abiramu. Ndipo m'gulu mwao mudayaka moto; lawi lake lidapsereza oipawo. Anapanga mwanawang'ombe ku Horebu, nagwadira fano loyenga. M'mwemo anasintha ulemerero wao ndi fanizo la ng'ombe yakudya msipu. Anaiwala Mulungu Mpulumutsi wao, amene anachita zazikulu m'Ejipito; zodabwitsa m'dziko la Hamu, zoopsa ku Nyanja Yofiira. Potero Iye adati awaononge, pakadapanda Mose wosankhika wake, kuima pamaso pake pogamukapo, kubweza ukali wake ungawaononge. Anapeputsanso dziko lofunika, osavomereza mau ake; koma anadandaula m'mahema mwao, osamvera mau a Yehova. Potero anawasamulira dzanja lake, kuti awagwetse m'chipululu: Kugwetsanso mbeu zao mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa m'maiko maiko. Ndipo anadziphatikiza ndi Baala-Peori, nadyanso nsembe za akufa. Ndipo anamkwiyitsa nazo zochita zao; kotero kuti mliri unawagwera. Pamenepo panauka Finehasi, nachita chilango: Ndi mliriwo unaletseka. Ndipo adamuyesa iye wachilungamo, ku mibadwomibadwo kunthawi zonse. Anautsanso mkwiyo wake kumadzi a Meriba, ndipo kudaipira Mose chifukwa cha iwowa: Pakuti anawawitsa mzimu wake, ndipo analankhula zosayenera ndi milomo yake. Sanaononga mitunduyo ya anthu, imene Yehova adawauza; koma anasokonekerana nao amitundu, naphunzira ntchito zao: Ndipo anatumikira mafano ao, amene anawakhalira msampha: Ndipo anapereka ana ao aamuna ndi aakazi nsembe ya kwa ziwanda, nakhetsa mwazi wosachimwa, ndiwo mwazi wa ana ao aamuna ndi aakazi, amene anawaperekera nsembe mafano a Kanani; m'mwemo analidetsa dziko ndi mwaziwo. Ndipo anadziipsa nazo ntchito zao, nachita chigololo nao machitidwe ao. Potero udayaka mkwiyo wa Yehova pa anthu ake, nanyansidwa Iye ndi cholowa chake. Ndipo anawapereka m'manja a amitundu; ndipo odana nao anachita ufumu pa iwo. Adani ao anawasautsanso, nawagonjetsa agwire mwendo wao. Iye anawalanditsa kawirikawiri; koma anapikisana ndi Iye mwa uphungu wao, ndi mphulupulu zao zinawafoketsa. Koma anapenya nsautso yao, pakumva kufuula kwao: Ndipo anawakumbukira chipangano chake, naleza monga mwa kuchuluka kwa chifundo chake. Ndipo anawachitira kuti apeze nsoni pamaso pa onse amene adawamanga ndende. Tipulumutseni, Yehova, Mulungu wathu, ndi kutisokolotsa kwa amitundu, kuti tiyamike dzina lanu loyera, ndi kudzitamandira nacho chilemekezo chanu. Wodala Yehova, Mulungu wa Israele, kuyambira kosayamba kufikira kosatha. Ndi anthu onse anene, Amen. Aleluya. Yamikani Yehova pakuti Iye ndiye wabwino; pakuti chifundo chake nchosatha. Atere oomboledwa a Yehova, amene anawaombola m'dzanja la wosautsa; nawasokolotsa kumaiko, kuchokera kum'mawa ndi kumadzulo, kumpoto ndi kunyanja. Anasokera m'chipululu, m'njira yopanda anthu; osapeza mudzi wokhalamo. Anamva njala ndi ludzu, moyo wao unakomoka m'kati mwao. Pamenepo anafuulira kwa Yehova mumsauko mwao, ndipo anawalanditsa m'kupsinjika kwao. Ndipo anawatsogolera pa njira yolunjika, kuti amuke kumudzi wokhalamo. Ayamike Yehova chifukwa cha chifundo chake, ndi zodabwitsa zake za kwa ana a anthu! Pakuti akhutitsa mtima wolakalaka, nadzaza mtima wanjala ndi zabwino. Iwo akukhala mumdima ndi mu mthunzi wa imfa, omangika ndi kuzunzika ndi chitsulo; popeza anapikisana nao mau a Mulungu, napeputsa uphungu wa Wam'mwambamwamba; kotero kuti anagonjetsa mtima wao ndi chovuta; iwowa anakhumudwa koma panalibe mthandizi. Pamenepo anafuulira kwa Yehova mumsauko mwao, ndipo anawapulumutsa m'kupsinjika kwao. Anawatulutsa mumdima ndi mu mthunzi wa imfa, nadula zomangira zao. Ayamike Yehova chifukwa cha chifundo chake, ndi zodabwitsa zake za kwa ana a anthu! Popeza adaswa zitseko zamkuwa, nathyola mipiringidzo yachitsulo. Anthu opusa azunzika chifukwa cha zolakwa zao, ndi chifukwa cha mphulupulu zao. Mtima wao unyansidwa nacho chakudya chilichonse; ndipo ayandikira zipata za imfa. Pamenepo afuulira kwa Yehova m'kusauka kwao, ndipo awapulumutsa m'kupsinjika kwao. Atumiza mau ake nawachiritsa, nawapulumutsa ku chionongeko chao. Ayamike Yehova chifukwa cha chifundo chake, ndi zodabwitsa zake za kwa ana a anthu! Ndipo apereke nsembe zachiyamiko, nafotokozere ntchito zake ndi kufuula mokondwera. Iwo akutsikira kunyanja nalowa m'zombo, akuchita ntchito zao pa madzi aakulu. Iwowa apenya ntchito za Yehova, ndi zodabwitsa zake m'madzi ozama. Popeza anena, nautsa namondwe, amene autsa mafunde ake. Akwera kuthambo, atsikira kozama; mtima wao usungunuka nacho choipacho. Adzandira napambanitsa miyendo ngati munthu woledzera, nathedwa nzeru konse. Pamenepo afuulira kwa Yehova m'kusauka kwao, ndipo awatulutsa m'kupsinjika kwao. Asanduliza namondwe akhale bata, kotero kuti mafunde ake atonthole. Pamenepo akondwera, popeza pagwa bata; ndipo Iye awatsogolera kudooko afunako. Ayamike Yehova chifukwa cha chifundo chake, ndi zodabwitsa zake za kwa ana a anthu! Amkwezenso mu msonkhano wa anthu, namlemekeze pokhala akulu. Asanduliza mitsinje ikhale chipululu, ndi akasupe a madzi akhale nthaka youma. Dziko la zipatso, likhale lakhulo, chifukwa cha choipa cha iwo okhalamo. Asanduliza chipululu chikhale thawale, ndi dziko louma likhale akasupe a madzi. Ndi apo akhalitsa anjala, kuti amangeko mudzi wokhalamo anthu; nafese m'minda, naoke mipesa, ndiyo yakubala zipatso zolemeza. Ndipo awadalitsa, kotero kuti achuluka kwambiri; osachepsanso zoweta zao. Koma achepanso, nawerama, chifukwa cha chisautso, choipa ndi chisoni. Atsanulira chimpepulo pa akulu, nawasokeretsa m'chipululu mopanda njira. Koma aika waumphawi pamsanje posazunzika, nampatsa mabanja ngati gulu la nkhosa. Oongoka mtima adzachiona nadzasekera; koma chosalungama chonse chitseka pakamwa pake. Wokhala nazo nzeru asamalire izi, ndipo azindikire zachifundo za Yehova. Nyimbo. Salimo la Davide. Wakhazikika mtima wanga, Mulungu; ndidzaimba, inde ndidzaimba zolemekeza, ndiko ulemerero wanga. Galamukani, chisakasa ndi zeze; ndidzauka ndekha mamawa. Ndidzakuyamikani mwa mitundu ya anthu, Yehova: ndipo ndidzaimba zakukulemekezani mwa anthu. Pakuti chifundo chanu nchachikulu kupitirira kumwamba, ndi choonadi chanu kufikira mitambo. Kwezekani pamwamba pa thambo, Mulungu; ndi ulemerero wanu pamwamba pa dziko lonse lapansi, kuti okondedwa anu alanditsidwe, pulumutsani ndi dzanja lanu lamanja ndipo mutivomereze. Mulungu analankhula m'chiyero chake; ndidzakondwerera: ndidzagawa Sekemu; ndidzayesa muyeso chigwa cha Sukoti. Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanga; ndi Efuremu ndiye mphamvu ya mutu wanga; Yuda ndiye wolamulira wanga. Mowabu ndiye mkhate wanga; pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga; ndidzafuulira Filistiya. Adzandifikitsa ndani m'mudzi wa m'linga? Adzanditsogolera ndani ku Edomu? Si ndinu Mulungu, amene mwatitaya osatuluka nao magulu athu? Tithandizeni mumsauko; pakuti chipulumutso cha munthu ndi chabe. Mwa Mulungu tidzachita molimbika mtima: Ndipo Iye adzapondereza otisautsa. Kwa Mkulu wa Nyimbo; Salimo la Davide. Mulungu wa chilemekezo changa, musakhale chete; pakuti pakamwa pa woipa ndi pakamwa pa chinyengo pananditsegukira; anandilankhulira ndi m'kamwa mwa bodza. Ndipo anandizinga ndi mau a udani, nalimbana nane kopanda chifukwa. M'malo mwa chikondi changa andibwezera udani; koma ine, kupemphera ndiko. Ndipo anandisenza choipa m'malo mwa chokoma, ndi udani m'malo mwa chikondi changa. Muike munthu woipa akhale mkulu wake; ndi mdani aime pa dzanja lamanja lake. Ponenedwa mlandu wake atuluke wotsutsika; ndi pemphero lake likhale ngati kuchimwa. Masiku ake akhale owerengeka; wina alandire udindo wake. Ana ake akhale amasiye, ndi mkazi wake wamasiye. Ana ake akhale amchirakuyenda ndi opemphapempha; afunefune zosowa zao kuchokera m'mabwinja mwao. Wokongoletsa agwire zonse ali nazo; ndi alendo alande za ntchito yake. Pasakhale munthu wakumchitira chifundo; kapena kuchitira chokoma ana ake amasiye. Zidzukulu zake zidulidwe; dzina lao lifafanizidwe mu mbadwo ukudza. Mphulupulu za makolo ake zikumbukike ndi Yehova; ndi tchimo la mai wake lisafafanizidwe. Zikhale pamaso pa Yehova chikhalire, kuti adule chikumbukiro chao kuchichotsera kudziko lapansi. Chifukwa kuti sanakumbukire kuchita chifundo, koma analondola wozunzika ndi waumphawi, ndi wosweka mtima, kuti awaphe. Inde, anakonda kutemberera, ndipo kudamdzera mwini; sanakondwere nako kudalitsa, ndipo kudamkhalira kutali. Anavalanso temberero ngati malaya, ndipo lidamlowa m'kati mwake ngati madzi, ndi ngati mafuta m'mafupa ake. Limkhalire ngati chovala adzikuta nacho, ndi lamba limene adzimangirira nalo m'chuuno chimangirire. Ichi chikhale mphotho ya otsutsana nane yowapatsa Yehova, ndi ya iwo akunenera choipa moyo wanga. Koma Inu, Yehova Ambuye, muchite nane chifukwa cha dzina lanu; ndilanditseni popeza chifundo chanu ndi chabwino. Pakuti ine ndine wozunzika ndi waumphawi, ndi mtima wanga walaswa m'kati mwanga. Ndamuka ngati mthunzi womka m'tali; ndiingidwa kwina ndi kwina ngati dzombe. Mabondo anga agwedezeka chifukwa cha kusala; ndi mnofu wanga waonda posowa mafuta. Ndiwakhaliranso chotonza; pakundiona apukusa mutu. Ndithandizeni Yehova, Mulungu wanga: Ndipulumutseni monga mwa chifundo chanu; kuti adziwe kuti ichi ndi dzanja lanu; kuti Inu Yehova munachichita. Atemberere iwowa, koma mudalitse ndinu; pakuuka iwowa adzachita manyazi, koma mtumiki wanu adzakondwera. Otsutsana nane avale manyazi, nadzikute nacho chisokonezo chao ngati ndi chofunda. Ndidzayamika Yehova kwakukulu pakamwa panga; ndi pakati pa anthu aunyinji ndidzamlemekeza. Popeza adzaima pa dzanja lamanja la waumphawi, kumpulumutsa kwa iwo akuweruza koipa moyo wake. Salimo la Davide. Yehova ananena kwa Ambuye wanga, Khalani pa dzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu. Yehova adzatumiza ndodo ya mphamvu yanu kuchokera ku Ziyoni; chitani ufumu pakati pa adani anu. Anthu anu adzadzipereka eni ake tsiku la chamuna chanu: M'moyera mokometsetsa, mobadwira matanda kucha, muli nao mame a ubwana wanu. Yehova walumbira, ndipo sadzasintha, Inu ndinu wansembe kosatha monga mwa chilongosoko cha Melkizedeki. Yehova pa dzanja lamanja lako adzaphwanya mafumu tsiku la mkwiyo wake. Adzaweruza mwa amitundu, adzadzaza dziko ndi mitembo; adzaphwanya mitu m'maiko ambiri. Adzamwa kumtsinje wa panjira; chifukwa chake adzaweramutsa mutu wake. Aleluya. Ndidzayamika Yehova ndi mtima wonse, mu upo wa oongoka mtima, ndi mumsonkhano. Ntchito za Yehova nzazikulu, zofunika ndi onse akukondwera nazo. Chochita Iye ncha ulemu, ndi ukulu: Ndi chilungamo chake chikhalitsa kosatha. Anachita chokumbukitsa zodabwitsa zake; Yehova ndiye wachisomo ndi nsoni zokoma. Anapatsa akumuopa Iye chakudya; adzakumbukira chipangano chake kosatha. Anaonetsera anthu ake mphamvu ya ntchito zake, pakuwapatsa cholowa cha amitundu. Ntchito za manja ake ndizo choonadi ndi chiweruzo; malangizo ake onse ndiwo okhulupirika. Achirikizika kunthawi za nthawi, achitika m'choonadi ndi chilunjiko. Anatumizira anthu ake chipulumutso; analamulira chipangano chake kosatha; dzina lake ndilo loyera ndi loopedwa. Kumuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru; onse akuchita chotero ali nacho chidziwitso chokoma; chilemekezo chake chikhalitsa kosatha. Aleluya. Wodala munthu wakuopa Yehova, wakukondwera kwambiri ndi malamulo ake. Mbeu yake idzakhala yamphamvu pa dziko lapansi; mbadwo wa oongoka mtima udzadalitsidwa. M'nyumba mwake mudzakhala akatundu ndi chuma: Ndi chilungamo chake chikhala chikhalire. Kuunika kutulukira oongoka mtima mumdima; Iye ndiye wachisomo, ndi wansoni ndi wolungama. Wodala munthu wakuchitira chifundo, nakongoletsa; adzalimbika nao mlandu wake poweruzidwa. Popeza sadzagwedezeka nthawi zonse; wolungama adzakumbukika ku nthawi yosatha. Sadzaopa mbiri yoipa; mtima wake ngwokhazika, wokhulupirira Yehova. Mtima wake ngwochirikizika, sadzachita mantha, kufikira ataona chofuna iye pa iwo omsautsa. Anagawagawa, anapatsa aumphawi; chilungamo chake chikhalitsa kosatha; nyanga yake idzakwezeka ndi ulemu. Woipa adzaziona, nadzapsa mtima; adzakukuta mano, nadzasungunuka; chokhumba oipa chidzatayika. Aleluya; Lemekezani, inu atumiki a Yehova; lemekezani dzina la Yehova. Lodala dzina la Yehova Kuyambira tsopano kufikira kosatha. Chitulukire dzuwa kufikira kulowa kwake lilemekezedwe dzina la Yehova. Yehova akwezeka pamwamba pa amitundu onse, ulemerero wake pamwambamwamba. Akunga Yehova Mulungu wathu ndani? Amene akhala pamwamba patali, nadzichepetsa apenye zam'mwamba ndi za pa dziko lapansi. Amene autsa wosauka kumchotsa kufumbi, nakweza waumphawi kumchotsa kudzala. Kuti amkhalitse pamodzi ndi akulu, pamodzi ndi akulu a anthu ake. Asungitsa nyumba mkazi wosaona mwana, akhale mai wokondwera ndi ana. Aleluya. M'mene Israele anatuluka ku Ejipito, nyumba ya Yakobo kwa anthu a chinenedwe chachilendo; Yuda anakhala malo ake oyera, Israele ufumu wake. Nyanjayo inaona, nithawa; Yordani anabwerera m'mbuyo. Mapiri anatumphatumpha ngati nkhosa zamphongo, timapiri ngati anaankhosa. Unathawanji nawe, nyanja iwe? Unabwereranji m'mbuyo, Yordani iwe? Munatumphatumphiranji ngati nkhosa zamphongo, mapiri inu? Ngati anaankhosa, zitunda inu? Unjenjemere, dziko lapansi iwe, pamaso pa Ambuye, pamaso pa Mulungu wa Yakobo; amene anasanduliza thanthwe likhale thawale lamadzi, nsangalabwi ikhale kasupe wamadzi. Kwa ife ai, Yehova, kwa ife ai, koma kwa dzina lanu patsani ulemerero, chifukwa cha chifundo chanu, ndi choonadi chanu. Aneneranji amitundu, Ali kuti Mulungu wao? Koma Mulungu wathu ndiye ali m'mwamba; achita chilichonse chimkonda. Mafano ao ndiwo a siliva ndi golide, ntchito za manja a anthu. Pakamwa ali napo, koma osalankhula; maso ali nao, koma osapenya; makutu ali nao, koma osamva; mphuno ali nazo, koma osanunkhiza; manja ali nao, koma osagwira; mapazi ali nao, koma osayenda; kapena sanena pammero pao. Adzafanana nao iwo akuwapanga; ndi onse akuwakhulupirira. Israele, khulupirira Yehova: Ndiye mthandizi wao ndi chikopa chao. Nyumba ya Aroni, khulupirira Yehova: Ndiye mthandizi wao, ndi chikopa chao. Inu akuopa Yehova, khulupirirani Yehova; ndiye mthandizi wao ndi chikopa chao. Yehova watikumbukira; adzatidalitsa: adzadalitsa nyumba ya Israele; adzadalitsa nyumba ya Aroni. Adzadalitsa iwo akuopa Yehova, aang'ono ndi aakulu. Yehova akuonjezereni dalitso, inu ndi ana anu. Odalitsika inu a kwa Yehova, wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi. Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova; koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu. Akufa salemekeza Yehova, kapena aliyense wakutsikira kuli chete: Koma ife tidzalemekeza Yehova kuyambira tsopano kufikira nthawi yonse. Aleluya. Ndimkonda, popeza Yehova amamva mau anga ndi kupemba kwanga. Popeza amanditcherera khutu lake, chifukwa chake ndidzaitanira Iye masiku anga onse. Zingwe za imfa zinandizinga, ndi zowawa za manda zinandigwira: ndinapeza nsautso ndi chisoni. Pamenepo ndinaitana dzina la Yehova; ndikuti, Yehova ndikupemphani landitsani moyo wanga. Yehova ngwa chifundo ndi wolungama; ndi Mulungu wathu ngwa nsoni. Yehova asunga opusa; ndidafooka ine, koma anandipulumutsa. Ubwere moyo wanga ku mpumulo wako; pakuti Yehova anakuchitira chokoma. Pakuti munalanditsa moyo wanga kuimfa, maso anga kumisozi, mapazi anga, ndingagwe. Ndidzayenda pamaso pa Yehova m'dziko la amoyo. Ndinakhulupirira, chifukwa chake ndinalankhula; ndinazunzika kwambiri. Pofulumizidwa mtima ndinati ine, anthu onse nga mabodza. Ndidzabwezera Yehova chiyani chifukwa cha zokoma zake zonse anandichitira? Ndidzanyamula chikho cha chipulumutso, ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova. Ndidzachita zowinda zanga za kwa Yehova, tsopano, pamaso pa anthu ake onse. Imfa ya okondedwa ake nja mtengo wake pamaso pa Yehova. Ndiloleni, Yehova, indetu ndine mtumiki wanu; ndine mtumiki wanu, mwana wa mdzakazi wanu; mwandimasulira zondimanga. Ndidzapereka kwa Inu nsembe yachiyamiko, ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova. Ndidzachita zowinda zanga za kwa Yehova, tsopano, pamaso pa anthu ake onse. M'mabwalo a nyumba ya Yehova, pakati pa inu, Yerusalemu. Aleluya. Lemekezani Yehova, amitundu onse; muimbireni, anthu onse. Pakuti chifundo chake cha pa ife ndi chachikulu; ndi choonadi cha Yehova nchosatha. Aleluya. Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino; pakuti chifundo chake nchosatha. Anene tsono Israele, kuti chifundo chake nchosatha. Anene tsono nyumba ya Aroni, kuti chifundo chake nchosatha. Anene tsono iwo akuopa Yehova, kuti chifundo chake nchosatha. M'mene ndinasautsika ndinaitanira pa Yehova; anandiyankha nandiika motakasuka Yehova. Yehova ndi wanga; sindidzaopa; adzandichitanji munthu? Yehova ndi wanga, mwa iwo akundithandiza; m'mwemo ndidzaona chofuna ine pa iwo akundida. Kuthawira kwa Yehova nkokoma koposa kukhulupirira munthu. Kuthawira kwa Yehova nkokoma koposa kukhulupirira akulu. Amitundu onse adandizinga, zedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula. Adandizinga, inde, adandizinga: Indedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula. Adandizinga ngati njuchi; anazima ngati moto waminga; indedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula. Kundikankha anandikankha ndikadagwa; koma Yehova anandithandiza. Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga; ndipo anakhala chipulumutso changa. M'mahema a olungama muli liu lakufuula mokondwera Dzanja lamanja la Yehova ndi la chipulumutso: Dzanja lamanja la Yehova likwezeka, Dzanja lamanja la Yehova lichita mwamphamvu. Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo, ndipo ndidzafotokozera ntchito za Yehova. Kulanga anandilangadi Yehova: koma sanandipereke kuimfa ai. Nditsegulireni zipata za chilungamo; ndidzalowamo, ndidzayamika Yehova. Chipata cha Yehova ndi ichi; olungama adzalowamo. Ndidzakuyamikani, popeza munandiyankha, ndipo munakhala chipulumutso changa. Mwala umene omangawo anaukana wakhala mutu wa pangodya. Ichi chidzera kwa Yehova; nchodabwitsa ichi pamaso pathu. Tsiku ili ndilo adaliika Yehova; tidzasekera ndi kukondwera m'mwemo. Tikupemphani, Yehova, tipulumutseni tsopano; tikupemphani, Yehova, tipindulitseni tsopano. Wodala wakudzayo m'dzina la Yehova; takudalitsani kochokera m'nyumba ya Yehova. Yehova ndiye Mulungu, amene anatiunikira; mangani nsembe ndi zingwe, kunyanga za guwa la nsembe. Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakuyamikani; ndinu Mulungu wanga, ndidzakukwezani. Yamikani Yehova, pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti chifundo chake nchosatha. Odala angwiro m'mayendedwe ao, akuyenda m'chilamulo cha Yehova. Odala iwo akusunga mboni zake, akumfuna ndi mtima wonse; inde, sachita chosalungama; ayenda m'njira zake. Inu munatilamulira, tisamalire malangizo anu ndi changu. Ha? Mwenzi zitakhazikika njira zanga kuti ndisamalire malemba anu. Pamenepo sindidzachita manyazi, pakupenyerera malamulo anu onse. Ndidzakuyamikani ndi mtima woongoka, pakuphunzira maweruzo anu olungama. Ndidzasamalira malemba anu: Musandisiye ndithu. Mnyamata adzayeretsa mayendedwe ake bwanji? Akawasamalira monga mwa mau anu. Ndinakufunani ndi mtima wanga wonse; ndisasokere kusiyana nao malamulo anu. Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu. Inu ndinu wodala Yehova; ndiphunzitseni malemba anu. Ndinafotokozera ndi milomo yanga maweruzo onse a pakamwa panu. Ndinakondwera m'njira ya mboni zanu, koposa ndi chuma chonse. Ndidzalingirira pa malangizo anu, ndi kupenyerera mayendedwe anu. Ndidzadzikondweretsa nao malemba anu; sindidzaiwala mau anu. Muchitire chokoma mtumiki wanu kuti ndikhale ndi moyo; ndipo ndidzasamalira mau anu. Munditsegulire maso, kuti ndipenye zodabwitsa za m'chilamulo chanu. Ine ndine mlendo pa dziko lapansi; musandibisire malamulo anu. Mtima wanga wasweka ndi kukhumba maweruzo anu nyengo zonse. Munadzudzula odzikuza otembereredwa, iwo akusokera kusiyana nao malamulo anu. Mundichotsere chotonza, ndi chimpepulo; pakuti ndinasunga mboni zanu. Nduna zomwe zinakhala zondineneza; koma mtumiki wanu analingirira malemba anu. Mboni zanu zomwe ndizo zondikondwetsa, ndizo zondipangira nzeru. Moyo wanga umamatika ndi fumbi; mundipatse moyo monga mwa mau anu. Ndinafotokozera njira zanga, ndipo munandiyankha: Mundiphunzitse malemba anu. Mundizindikiritse njira ya malangizo anu; kuti ndilingalire zodabwitsa zanu. Moyo wanga wasungunuka ndi chisoni: Mundilimbitse monga mwa mau anu. Mundichotsere njira ya chinyengo; nimundipatse mwachifundo chilamulo chanu. Ndinasankha njira yokhulupirika; ndinaika maweruzo anu pamaso panga. Ndimamatika nazo mboni zanu; musandichititse manyazi, Yehova. Ndidzathamangira njira ya malamulo anu, mutakulitsa mtima wanga. Mundiphunzitse, Yehova, njira ya malemba anu; ndidzaisunga kufikira kutha kwake. Mundizindikiritse, ndipo ndidzasunga malamulo anu; ndidzawasamalira ndi mtima wanga wonse. Mundiyendetse mopita malamulo anu; pakuti ndikondwera m'menemo. Lingitsani mtima wanga kumboni zanu, si ku chisiriro ai. Muchititse mlubza maso anga ndisapenye zachabe, mundipatse moyo mu njira yanu. Limbitsirani mtumiki wanu mau anu, ndiye wodzipereka kukuopani. Mundipatutsire chotonza changa ndichiopacho; popeza maweruzo anu ndi okoma. Taonani, ndinalira malangizo anu; mundipatse moyo mwa chilungamo chanu. Ndipo chifundo chanu chindidzere, Yehova, ndi chipulumutso chanu, monga mwa mau anu. Kuti ndikhale nao mau akuyankha wonditonza; popeza ndikhulupirira mau anu. Ndipo musandichotsere ndithu mau a choonadi pakamwa panga; pakuti ndinayembekeza maweruzo anu. Potero ndidzasamalira malamulo anu chisamalire kunthawi za nthawi. Ndipo ndidzayenda mwaufulu; popeza ndinafuna malangizo anu. Ndidzalankhulanso za umboni wanu pamaso pa mafumu, osachitapo manyazi. Ndipo ndidzadzikondweretsa nao malamulo anu, amene ndiwakonda. Ndidzakwezanso manja anga ku malamulo anu, amene ndiwakonda; ndipo ndidzalingalira pa malemba anu. Kumbukirani mau a kwa mtumiki wanu, amene munandiyembekezetsa nao. Chitonthozo changa m'kuzunzika kwanga ndi ichi; pakuti mau anu anandipatsa moyo. Odzikuza anandinyoza kwambiri: koma sindinapatukanso nacho chilamulo chanu. Ndinakumbukira maweruzo anu kuyambira kale, Yehova, ndipo ndinadzitonthoza. Ndinasumwa kwakukulu, chifukwa cha oipa akusiya chilamulo chanu. Malemba anu anakhala nyimbo zanga m'nyumba ya ulendo wanga. Usiku ndinakumbukira dzina lanu, Yehova, ndipo ndinasamalira chilamulo chanu. Ichi ndinali nacho, popeza ndinasunga malangizo anu. Yehova ndiye gawo langa: Ndinati ndidzasunga mau anu. Ndinapemba pankhope panu ndi mtima wanga wonse: Mundichitire chifundo monga mwa mau anu. Ndinaganizira njira zanga, ndipo ndinabweza mapazi anga atsate mboni zanu. Ndinafulumira, osachedwa, kusamalira malamulo anu. Anandikulunga nazo zingwe za oipa; koma sindinaiwala chilamulo chanu. Pakati pa usiku ndidzauka kukuyamikani chifukwa cha maweruzo anu olungama. Ine ndine wakuyanjana nao onse akukuopani, ndi iwo akusamalira malangizo anu. Dziko lapansi lidzala nacho chifundo chanu, Yehova; mundiphunzitse malemba anu. Munachitira mtumiki wanu chokoma, Yehova, monga mwa mau anu. Mundiphunzitse chisiyanitso ndi nzeru; pakuti ndinakhulupirira malamulo anu. Ndisanazunzidwe ndinasokera; koma tsopano ndisamalira mau anu. Inu ndinu wabwino, ndi wakuchita zabwino; mundiphunzitse malemba anu. Odzikuza anandipangira bodza: Ndidzasunga malangizo anu ndi mtima wanga wonse. Mtima wao unona ngati mafuta; koma ine ndikondwera nacho chilamulo chanu. Kundikomera kuti ndinazunzidwa; kuti ndiphunzire malemba anu. Chilamulo cha pakamwa panu chindikomera koposa golide ndi siliva zikwizikwi. Manja anu anandilenga nandiumba; mundizindikiritse, kuti ndiphunzire malemba anu. Iwo amene akuopani adzandiona ine nadzakondwera; popeza ndayembekezera mau anu. Ndidziwa kuti maweruzo anu ndiwo olungama, Yehova, ndi kuti munandizunza ine mokhulupirika. Chifundo chanu chikhaletu chakunditonthoza, ndikupemphani, monga mwa mau anu kwa mtumiki wanu. Nsoni zokoma zanu zindidzere, kuti ndikhale ndi moyo; popeza chilamulo chanu chindikondweretsa. Odzikuza achite manyazi, popeza anandichitira monyenga ndi bodza: Koma ine ndidzalingalira malangizo anu. Iwo akuopa Inu abwere kwa ine, ndipo adzadziwa mboni zanu. Mtima wanga ukhale wangwiro m'malemba anu; kuti ndisachite manyazi. Moyo wanga unakomoka ndi kukhumba chipulumutso chanu: Ndinayembekezera mau anu. Maso anga anatha mphamvu ndi kukhumba mau anu, ndikuti, Mudzanditonthoza liti? Popeza ndakhala ngati thumba lofukirira; koma sindiiwala malemba anu. Masiku a mtumiki wanu ndiwo angati? Mudzaweruza liti iwo akundilondola koipa? Odzikuza anandikumbira mbuna, ndiwo osasamalira chilamulo chanu. Malamulo anu onse ngokhulupirika; andilondola nalo bodza; ndithandizeni. Akadandithera pa dziko lapansi; koma ine sindinasiya malangizo anu. Mundipatse moyo monga mwa chifundo chanu; ndipo ndidzasamalira mboni ya pakamwa panu. Mau anu aikika kumwamba, kosatha, Yehova. Chikhulupiriko chanu chifikira mibadwomibadwo; munakhazikitsa dziko lapansi, ndipo likhalitsa. Kunena za maweruzo anu alimbikira kufikira lero; pakuti onsewa ndiwo atumiki anu. Chilamulo chanu chikadapanda kukhala chikondweretso changa, ndikadatayika m'kuzunzika kwanga. Sindidzaiwala malangizo anu nthawi zonse; popeza munandipatsa nao moyo. Ine ndine wanu, ndipulumutseni pakuti ndinafuna malangizo anu. Oipa anandilalira kundiononga; koma ndizindikira mboni zanu. Ndinapenya malekezero ake a ungwiro wonse; koma lamulo lanu ndi lotakasuka ndithu. Ha! Ndikondadi chilamulo chanu; ndilingiriramo ine tsiku lonse. Malamulo anu andipatsa nzeru yakuposa adani anga; pakuti akhala nane chikhalire. Ndili nayo nzeru yakuposa aphunzitsi anga onse; pakuti ndilingalira mboni zanu. Ndizindikira koposa okalamba popeza ndinasunga malangizo anu. Ndinaletsa mapazi anga njira iliyonse yaoipa, kuti ndisamalire mau anu. Sindinapatukana nao maweruzo anu; pakuti Inu munandiphunzitsa. Mau anu azunadi powalawa ine! Koposa uchi m'kamwa mwanga. Malangizo anu andizindikiritsa; chifukwa chake ndidana nao mayendedwe onse achinyengo. Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga. Ndinalumbira, ndipo ndinatsimikiza mtima, kuti ndidzasamalira maweruzo anu olungama. Ndazunzika kwambiri: Ndipatseni moyo, Yehova, monga mwa mau anu. Landirani, Yehova, zopereka zaufulu za pakamwa panga, ndipo ndiphunzitseni maweruzo anu. Moyo wanga ukhala m'dzanja langa chikhalire; koma sindiiwala chilamulo chanu. Oipa ananditchera msampha; koma sindinasokera m'malangizo anu. Ndinalandira mboni zanu zikhale cholandira chosatha; pakuti ndizo zokondweretsa mtima wanga. Ndinalingitsa mtima wanga uchite malemba anu, kosatha, kufikira chimaliziro. Ndidana nao a mitima iwiri; koma ndikonda chilamulo chanu. Inu ndinu pobisalapo panga, ndi chikopa changa; ndiyembekezera mau anu. Mundichokere ochita zoipa inu; kuti ndisunge malamulo a Mulungu wanga. Mundichirikize monga mwa mau anu, kuti ndikhale ndi moyo; ndipo ndisachite manyazi pa chiyembekezo changa. Mundigwirizize ndipo ndidzapulumutsidwa, ndipo ndidzasamalira malemba anu chisamalire. Mupepula onse akusokera m'malemba anu; popeza chinyengo chao ndi bodza. Muchotsa oipa onse a pa dziko lapansi ngati mphala: Chifukwa chake ndikonda mboni zanu. Thupi langa linjenjemera ndi kuopa Inu; ndipo ndichita mantha nao maweruzo anu. Ndinachita chiweruzo ndi chilungamo; musandisiyira akundisautsa. Mumkhalire chikole mtumiki wanu chimkomere; odzikuza asandisautse. Maso anga anatha mphamvu pofuna chipulumutso chanu, ndi mau a chilungamo chanu. Muchitire mtumiki wanu monga mwa chifundo chanu, ndipo ndiphunzitseni malemba anu. Ine ndine mtumiki wanu, ndizindikiritseni; kuti ndidziwe mboni zanu. Yafika nyengo yakuti Yehova achite kanthu; pakuti anaswa chilamulo chanu. Chifukwa chake ndikonda malamulo anu koposa golide, inde golide woyengeka. Chifukwa chake ndiyesa ngolunjika malangizo anu onse akunena zonse; koma ndidana nazo njira zonse zonyenga. Mboni zanu nzodabwitsa; chifukwa chake moyo wanga uzisunga. Potsegulira mau anu paunikira; kuzindikiritsa opusa. Ndinatsegula pakamwa panga, ndi kupuma wefuwefu; popeza ndinakhumba malamulo anu. Munditembenukire, ndi kundichitira chifundo, monga mumatero nao akukonda dzina lanu. Khazikitsani mapazi anga m'mau anu; ndipo zisandigonjetse zopanda pake zilizonse. Mundiombole kunsautso ya munthu: Ndipo ndidzasamalira malangizo anu. Muwalitse nkhope yanu pa mtumiki wanu; ndipo mundiphunzitse malemba anu. Maso anga atsitsa mitsinje ya madzi, popeza sasamalira chilamulo chanu. Inu ndinu wolungama, Yehova, ndipo maweruzo anu ndiwo olunjika. Mboni zanuzo mudazilamulira zili zolungama ndi zokhulupirika ndithu. Changu changa chinandithera, popeza akundisautsa anaiwala mau anu. Mau anu ngoyera ndithu; ndi mtumiki wanu awakonda. Wamng'ono ine, ndi wopepulidwa; koma sindiiwala malemba anu. Chilungamo chanu ndicho chilungamo chosatha; ndi chilamulo chanu ndicho choonadi. Kusautsika ndi kupsinjika kwandigwera; koma malamulo anu ndiwo ondikondweretsa ine. Mboni zanu ndizo zolungama kosatha; mundizindikiritse izi, ndipo ndidzakhala ndi moyo. Ndinaitana ndi mtima wanga wonse; mundiyankhe, Yehova; ndidzasunga malemba anu. Ndinaitanira Inu; ndipulumutseni, ndipo ndidzasamalira mboni zanu. Ndinafuula kusanake: ndinayembekezera mau anu. Maso anga anakumana ndi maulonda a usiku, kuti ndilingirire mau anu. Imvani liu langa monga mwa chifundo chanu; mundipatse moyo monga mwa kuweruza kwanu, Yehova. Otsata zachiwembu andiyandikira; akhala kutali ndi chilamulo chanu. Inu muli pafupi, Yehova; ndipo malamulo anu onse ndiwo choonadi. Kuyambira kale ndinadziwa mu mboni zanu, kuti munazikhazika kosatha, Penyani kuzunzika kwanga, nimundilanditse; pakuti sindiiwala chilamulo chanu. Mundinenere mlandu wanga, nimundiombole; mundipatse moyo monga mwa mau anu. Chipulumutso chitalikira oipa; popeza safuna malemba anu. Zachifundo zanu ndi zazikulu, Yehova; mundipatse moyo monga mwa maweruzo anu. Ondilondola ndi ondisautsa ndiwo ambiri; koma sindinapatukana nazo mboni zanu. Ndinapenya ochita monyenga, ndipo ndinanyansidwa nao; popeza sasamalira mau anu. Penyani kuti ndikonda malangizo anu; mundipatse moyo, Yehova, monga mwa chifundo chanu. Chiwerengero cha mau anu ndicho choonadi; ndi maweruzo anu olungama onse akhala kosatha. Nduna zinandilondola kopanda chifukwa; koma mtima wanga uchita mantha nao mau anu. Ndikondwera nao mau anu, ngati munthu wakupeza zofunkha zambiri. Ndidana nalo bodza ndi kunyansidwa nalo; koma ndikonda chilamulo chanu. Ndikulemekezani kasanu ndi kawiri, tsiku limodzi, chifukwa cha maweruzo anu alungama. Akukonda chilamulo chanu ali nao mtendere wambiri; ndipo alibe chokhumudwitsa. Ndinayembekeza chipulumutso chanu, Yehova, ndipo ndinachita malamulo anu. Moyo wanga unasamalira mboni zanu; ndipo ndizikonda kwambiri. Ndinasamalira malangizo anu ndi mboni zanu; popeza njira zanga zonse zili pamaso panu. Kufuula kwanga kuyandikire pamaso panu, Yehova; mundizindikiritse monga mwa mau anu. Kupemba kwanga kudze pamaso panu; mundilanditse monga mwa mau anu. Milomo yanga itulutse chilemekezo; popeza mundiphunzitsa malemba anu. Lilime langa liimbire mau anu; pakuti malamulo anu onse ndiwo olungama. Dzanja lanu likhale lakundithandiza; popeza ndinasankha malangizo anu. Ndinakhumba chipulumutso chanu, Yehova; ndipo chilamulo chanu ndicho chondikondweretsa. Mzimu wanga ukhale ndi moyo, ndipo udzakulemekezani; ndipo maweruzo anu andithandize. Ndinasochera ngati nkhosa yotayika; funani mtumiki wanu; pakuti sindiiwala malamulo anu. Nyimbo yokwerera. Ndinafuulira kwa Yehova mu msauko wanga, ndipo anandivomereza. Yehova, landitsani moyo wanga kumilomo ya mabodza, ndi kulilime lonyenga. Adzakuninkhanji, adzakuonjezeranji, lilime lonyenga iwe? Mivi yakuthwa ya chiphona, ndi makala tsanya. Tsoka ine, kuti ndili mlendo m'Meseki, kuti ndigonera m'mahema a Kedara! Moyo wanga unakhalitsa nthawi pamodzi ndi iye wakudana nao mtendere. Ine ndikuti, Mtendere; koma polankhula ine, iwowa akuti, Nkhondo. Nyimbo yokwerera. Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti? Thandizo langa lidzera kwa Yehova, wakulenga zakumwamba ndi dziko lapansi. Sadzalola phazi lako literereke: Iye amene akusunga sadzaodzera. Taonani, wakusunga Israele sadzaodzera kapena kugona. Yehova ndiye wakukusunga; Yehova ndiye mthunzi wako wa kudzanja lako lamanja. Dzuwa silidzawamba usana, mwezi sudzakupanda usiku. Yehova adzakusunga kukuchotsera zoipa zilizonse; adzasunga moyo wako. Yehova adzasungira kutuluka kwako ndi kulowa kwako, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse. Nyimbo yokwerera; ya Davide. Ndinakondwera m'mene ananena nane, Tiyeni kunyumba ya Yehova. Mapazi athu alinkuima m'zipata zanu, Yerusalemu Yerusalemu anamangidwa ngati mudzi woundana bwino: Kumene akwerako mafuko, ndiwo mafuko a Yehova; akhale mboni ya kwa Israele, Ayamike dzina la Yehova. Pakuti pamenepo anaika mipando ya chiweruzo, mipando ya nyumba ya Davide. Mupempherere mtendere wa Yerusalemu; akukonda inu adzaona phindu. M'linga mwako mukhale mtendere, m'nyumba za mafumu mukhale phindu. Chifukwa cha abale anga ndi mabwenzi anga, ndidzanena tsopano, Mukhale mtendere mwa inu. Chifukwa cha nyumba ya Yehova Mulungu wathu ndidzakufunira zokoma. Nyimbo yokwerera. Ndikweza maso anga kwa Inu, kwa Inu wakukhala kumwamba. Taonani, monga maso a anyamata ayang'anira dzanja la mbuye wao, monga maso a adzakazi ayang'anira dzanja la mbuye wao wamkazi: Momwemo maso athu ayang'anira Yehova Mulungu wathu, kufikira atichitira chifundo. Mutichitire chifundo, Yehova, mutichitire chifundo; pakuti takhuta kwambiri ndi mnyozo. Moyo wathu wakhuta ndithu ndi kuseka kwa iwo osasowa kanthu, ndi mnyozo wa odzikuza. Nyimbo yokwerera; ya Davide. Akadapanda kukhala nafe Yehova, anene tsono Israele; Akadapanda kukhala nafe Yehova, pakutiukira anthu: Akadatimeza amoyo, potipsera mtima wao. Akadatimiza madziwo, mtsinje ukadapita pa moyo wathu; madzi odzikuza akadapita pa moyo wathu. Alemekezedwe Yehova, amene sanatipereke kumano kwao tikhale chakudya chao. Moyo wathu unaonjoka ngati mbalame mu msampha wa msodzi; msampha unathyoka ndi ife tinaonjoka. Thandizo lathu lili m'dzina la Yehova, wolenga kumwamba ndi dziko lapansi. Nyimbo yokwerera. Iwo akukhulupirira Yehova akunga phiri la Ziyoni, losasunthika, likhazikika kosatha. Monga mapiri azinga Yerusalemu, momwemo Yehova azinga anthu ake, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse. Pakuti ndodo yachifumu ya choipa siidzapumula pa gawo la olungama; kuti olungama asatulutse dzanja lao kuchita chosalungama. Chitirani chokoma, Yehova, iwo okhala okoma; iwo okhala oongoka mumtima mwao. Koma iwo akupatula kutsata njira zao zokhotakhota, Yehova adzawachotsa pamodzi ndi ochita zopanda pake. Mtendere ukhale pa Israele. Nyimbo yokwerera. Pobweza Yehova ukapolo wa Ziyoni, tinakhala ngati anthu akulota. Pamenepo pakamwa pathu panadzala ndi kuseka, ndi lilime lathu linafuula mokondwera; pamenepo anati mwa amitundu, Yehova anawachitira iwo zazikulu. Yehova anatichitira ife zazikulu; potero tikhala okondwera. Bwezani ukapolo wathu, Yehova, ngati mitsinje ya kumwera. Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kufuula mokondwera. Iye amene ayendayenda nalira, ponyamula mbeu yakufesa; adzabweranso ndithu ndi kufuula mokondwera, alikunyamula mitolo yake. Nyimbo yokwerera; ya Solomoni. Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe; akapanda kusunga mudzi Yehova, mlonda adikira chabe. Kuli chabe kwa inu kulawirira mamawa ndi kusagonerapo madzulo, kudya mkate wosautsa kuupeza; kuli tero kuti izi apatsa okondedwa ake ngati m'tulo. Taonani, ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova; chipatso cha m'mimba ndicho mphotho yake. Ana a ubwana wake wa munthu akunga mivi m'dzanja lake la chiphona. Wodala munthu amene anadzaza nayo phodo lake: sadzachita manyazi iwo, pakulankhula nao adani kuchipata. Nyimbo yokwerera. Wodala yense wakuopa Yehova, wakuyenda m'njira zake. Pakuti udzadya za ntchito ya manja ako; wodala iwe, ndipo kudzakukomera. Mkazi wako adzanga mpesa wopatsa m'mbali za nyumba yako; ana ako adzanga timitengo ta azitona pozinga podyera pako. Taonani, m'mwemo adzadalitsika munthu wakuopa Yehova. Yehova adzakudalitsa ali m'Ziyoni; ndipo udzaona zokoma za Yerusalemu masiku onse a moyo wako. Inde, udzaona zidzukulu zako. Mtendere ukhala ndi Israele. Nyimbo yokwerera. Anandisautsa kawirikawiri kuyambira ubwana wanga, anene tsono Israele; Anandisautsa kawirikawiri kuyambira ubwana wanga; koma sanandilake. Olima analima pamsana panga; anatalikitsa mipere yao. Yehova ndiye wolungama; anadulatu zingwe za oipa. Achite manyazi nabwerere m'mbuyo. Onse akudana naye Ziyoni. Akhale ngati udzu womera patsindwi, wakufota asanauzule; umene womweta sadzaza nao dzanja lake, kapena womanga mitolo sakupatira manja. Angakhale opitirirapo sanena, Dalitso la Mulungu likhale pa inu; tikudalitsani m'dzina la Yehova. Nyimbo yokwerera. M'mozamamo ndinakufuulirani, Yehova. Ambuye, imvani liu langa; makutu anu akhale chimverere mau a kupemba kwanga. Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chilili ndani, Ambuye? Koma kwa Inu kuli chikhululukiro, kuti akuopeni. Ndilindira Yehova, moyo wanga ulindira, ndiyembekeza mau ake. Moyo wanga uyang'anira Ambuye, koposa alonda matanda kucha; inde koposa alonda matanda kucha. Israele, uyembekezere Yehova; chifukwa kwa Yehova kuli chifundo, kwaonso kuchulukira chiombolo. Ndipo adzaombola Israele ku mphulupulu zake zonse. Nyimbo yokwerera, ya Davide. Yehova, mtima wanga sunadzikuze ndi maso anga sanakwezeke; ndipo sindinatsate zazikulu, kapena zodabwitsa zondiposa. Indedi, ndinalinganiza ndi kutontholetsa moyo wanga; ngati mwana womletsa kuyamwa amake, moyo wanga ndili nao ngati mwana womletsa kuyamwa. Israele, uyembekezere Yehova, kuyambira tsopano kufikira kosatha. Nyimbo yokwerera. Yehova, kumbukirani Davide kuzunzika kwake konse. Kuti analumbira Yehova, nawindira Wamphamvuyo wa Yakobo, ndi kuti, Ngati ndidzalowa pakhomo pa nyumba yanga, ngati ndidzakwera pa kama logonapo; ngati ndidzalola maso anga agone, kapena zikope zanga ziodzere; kufikira nditapezera Yehova malo, chokhalamo Wamphamvuyo wa Yakobo? Taonani, tinachimva m'Efurata; tinachipeza kuchidikha cha kunkhalango. Tidzalowa mokhalamo Iye; tidzagwadira kumpando wa mapazi ake. Ukani, Yehova, lowani ku mpumulo wanu; Inu ndi hema wa mphamvu yanu. Ansembe anu avale chilungamo; ndi okondedwa anu afuule mokondwera. Chifukwa cha Davide mtumiki wanu musabweze nkhope ya wodzozedwa wanu. Yehova analumbira Davide zoona; sadzalibweza; ndi kuti, Wa iwo okhala zipatso za thupi lako ndidzaika pa mpando wachifumu wako. Ana ako akasunga chipangano changa ndi mboni yanga imene ndidzawaphunzitsa, ana aonso adzakhala pa mpando wanu kunthawi zonse, pakuti Yehova anasankha Ziyoni; analikhumba likhale pokhala pake; ndi kuti, Pampumulo panga mpano posatha, Pano ndidzakhala; pakuti ndakhumbapo. Ndidzadalitsatu chakudya chake; aumphawi ake ndidzawakhutitsa ndi mkate. Ndipo ansembe ake ndidzawaveka ndi chipulumutso: Ndi okondedwa ake adzafuulitsa mokondwera. Apo ndidzaphukitsira Davide nyanga; ndakonzeratu wodzozedwa wanga nyali. Ndidzawaveka adani ake ndi manyazi; koma pa iyeyu korona wake adzamveka. Nyimbo yokwerera; ya Davide. Onani, nkokoma ndi kokondweretsa ndithu kuti abale akhale pamodzi! Ndiko ngati mafuta a mtengo wake pamutu, akutsikira kundevu, inde kundevu za Aroni; akutsikira kumkawo wa zovala zake. Ngati mame a ku Heremoni, akutsikira pa mapiri a Ziyoni. Pakuti pamenepo Yehova analamulira dalitsolo, ndilo moyo womka muyaya. Nyimbo yokwerera. Taonani, lemekezani Yehova, atumiki a Yehova inu nonse, akuimirira m'nyumba ya Yehova usiku. Kwezani manja anu kumalo oyera, nimulemekeze Yehova. Yehova, ali m'Ziyoni, akudalitseni; ndiye amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi. Aleluya; Lemekezani dzina la Yehova! Lemekezani inu atumiki a Yehova. Inu akuimirira m'nyumba ya Yehova, m'mabwalo a nyumba ya Mulungu wathu. Lemekezani Yehova; pakuti Yehova ndiye wabwino; muimbire zolemekeza dzina lake; pakuti nkokondweretsa kutero. Pakuti Yehova anadzisankhira Yakobo, Israele, akhale chuma chake chenicheni. Pakuti ndidziwa kuti Yehova ndi wamkulu, ndi Ambuye wathu aposa milungu yonse. Chilichonse chimkonda Yehova achichita, kumwamba ndi pa dziko lapansi, m'nyanja ndi mozama monse. Akweza mitambo ichokere ku malekezero a dziko lapansi; ang'animitsa mphezi zidzetse mvula; atulutsa mphepo mosungira mwake. Anapanda oyamba a Ejipito, kuyambira munthu kufikira zoweta. Anatumiza zizindikiro ndi zodabwitsa pakati pako, Ejipito iwe, pa Farao ndi pa omtumikira onse. Ndiye amene anapanda amitundu ambiri, napha mafumu amphamvu; Sihoni mfumu ya Aamori, ndi Ogi mfumu ya Basani, ndi maufumu onse a Kanani: Ndipo anapereka dziko lao likhale chosiyira, chosiyira cha kwa Israele anthu ake. Dzina lanu, Yehova, likhala kosatha; chikumbukiro chanu, Yehova, kufikira mibadwomibadwo. Pakuti Yehova adzaweruza anthu ake, koma adzaleka atumiki ake. Mafano a amitundu ndiwo siliva ndi golide, ntchito ya manja a anthu. Pakamwa ali napo koma osalankhula; maso ali nao, koma osapenya; makutu ali nao, koma osamva; inde, pakamwa pao palibe mpweya. Akuwapanga adzafanana nao; inde, onse akuwakhulupirira. A nyumba ya Israele inu, lemekezani Yehova: A nyumba ya Aroni inu, lemekezani Yehova: A nyumba ya Levi inu, lemekezani Yehova: Inu akuopa Yehova, lemekezani Yehova. Alemekezedwe Yehova kuchokera m'Ziyoni, amene akhala m'Yerusalemu. Aleluya. Yamikani Yehova pakuti ndiye wabwino; pakuti chifundo chake nchosatha. Yamikani Mulungu wa milungu; pakuti chifundo chake nchosatha. Yamikani Mbuye wa ambuye; pakuti chifundo chake nchosatha. Amene yekha achita zodabwitsa zazikulu; pakuti chifundo chake nchosatha. Amene analenga zakumwamba mwanzeru; pakuti chifundo chake nchosatha. Amene anayala dziko lapansi pamwamba pa madzi; pakuti chifundo chake nchosatha. Amene analenga miuni yaikulu; pakuti chifundo chake nchosatha. Dzuwa liweruze usana; pakuti chifundo chake nchosatha. Mwezi ndi nyenyezi ziweruze usiku; pakuti chifundo chake nchosatha. Iye amene anapandira Aejipito ana ao oyamba; pakuti chifundo chake nchosatha. Natulutsa Israele pakati pao; pakuti chifundo chake nchosatha. Ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka; pakuti chifundo chake nchosatha. Amene anagawa magawo Nyanja Yofiira; pakuti chifundo chake nchosatha. Napititsa Israele pakati pake; pakuti chifundo chake nchosatha. Nakhuthula Farao ndi khamu lake m'Nyanja Yofiira: pakuti chifundo chake nchosatha. Amene anatsogolera anthu ake m'chipululu; pakuti chifundo chake nchosatha. Amene anapanda mafumu akulu; pakuti chifundo chake nchosatha. Ndipo anawapha mafumu omveka; pakuti chifundo chake nchosatha. Sihoni mfumu ya Aamori; pakuti chifundo chake nchosatha. Ndi Ogi mfumu ya Basani; pakuti chifundo chake nchosatha. Ndipo anapereka dziko lao likhale chosiyira; pakuti chifundo chake nchosatha. Chosiyira cha kwa Israele mtumiki wake; pakuti chifundo chake nchosatha. Amene anatikumbukira popepuka ife; pakuti chifundo chake nchosatha. Natikwatula kwa otisautsa; pakuti chifundo chake nchosatha. Ndiye wakupatsa nyama zonse chakudya; pakuti chifundo chake nchosatha. Yamikani Mulungu wa kumwamba; pakuti chifundo chake nchosatha. Ku mitsinje ya ku Babiloni, kumeneko tinakhala pansi, inde tinalira, pokumbukira Ziyoni. Pa msondodzi uli m'mwemo tinapachika mazeze athu. Popeza pamenepo akutigwirawo anatifunsa nyimbo ndipo akutizunza anafuna tisekere, ndi kuti, Mutiimbire nyimbo imodzi ya ku Ziyoni. Tidati, Tidzaimba bwanji nyimbo ya Yehova m'dziko lachilendo? Ndikakuiwalani, Yerusalemu, dzanja lamanja langa liiwale luso lake. Lilime langa limamatike kunsaya zanga, ndikapanda kukumbukira inu; ndikapanda kusankha Yerusalemu koposa chimwemwe changa chopambana. Yehova, kumbukirani ana a Edomu tsiku la Yerusalemu; amene adati, Gamulani, gamulani, kufikira maziko ake. Mwana wamkazi wa ku Babiloni, iwe amene udzapasulidwa; wodala iye amene adzakubwezera chilango monga umo unatichitira ife. Wodala iye amene adzagwira makanda ako, ndi kuwaphwanya pathanthwe. Salimo la Davide. Ndidzakuyamikani ndi mtima wanga wonse; ndidzaimba zakukulemekezani patsogolo pa milungu. Ndidzagwadira kuloza ku Kachisi wanu woyera, ndi kuyamika dzina lanu, chifukwa cha chifundo chanu ndi choonadi chanu; popeza munakuzitsa mau anu koposa dzina lanu lonse. Tsiku loitana ine, munandiyankha, munandilimbitsa ndi mphamvu m'moyo mwanga. Mafumu onse a pa dziko lapansi adzakuyamikani, Yehova, popeza adamva mau a pakamwa panu. Ndipo adzaimbira njira za Yehova; pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu. Angakhale Yehova ngwokwezeka, apenyanso wopepukayo; koma wodzikuza amdziwira kutali. Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo; mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu, ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa. Yehova adzanditsirizira za kwa ine: Chifundo chanu, Yehova, chifikira kunthawi zonse: Musasiye ntchito za manja anu. Kwa Mkulu wa Nyimbo; Salimo la Davide. Munandisanthula, Yehova, nimundidziwa. Inu mudziwa kukhala kwanga ndi kuuka kwanga, muzindikira lingaliro langa muli kutali. Muyesa popita ine ndi pogona ine, ndi njira zanga zonse muzolowerana nazo. Pakuti asanafike mau pa lilime langa, taonani, Yehova, muwadziwa onse. Munandizinga kumbuyo ndi kumaso, nimunaika dzanja lanu pa ine. Kudziwa ichi kundilaka ndi kundidabwitsa: Kundikhalira patali, sindifikirako. Ndidzapita kuti kuzembera mzimu wanu? Kapena ndidzathawira kuti kuzembera nkhope yanu? Ndikakwera kunka kumwamba, muli komweko; kapena ndikadziyalira ku Gehena, taonani, muli komweko. Ndikadzitengera mapiko a mbandakucha, ndi kukhala ku malekezero a nyanja; kungakhale komweko dzanja lanu lidzanditsogolera, nilidzandigwira dzanja lanu lamanja. Ndipo ndikati, Koma mdima undiphimbe, ndi kuunika kondizinga kukhale usiku. Ungakhale mdima sudetsa pamaso panu, koma usiku uwala ngati usana; mdima ukunga kuunika. Pakuti Inu munalenga impso zanga; munandiumba ndisanabadwe ine. Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu. Thupi langa silinabisikira Inu popangidwa ine mobisika, poombedwa ine monga m'munsi mwake mwa dziko lapansi. Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya, ziwalo zanga zonse zinalembedwa m'buku mwanu, masiku akuti ziumbidwe, pakalibe chimodzi cha izo. Potero, Mulungu, ndiziyesa zolingalira zanu za mtengo wake ndithu! Mawerengedwe ake ndi ambirimbiri! Ndikaziwerenga zichuluka koposa mchenga: Ndikauka ndikhalanso nanu. Indedi, mudzaomba woipa, Mulungu: Ndipo amuna inu okhumba mwazi, chokani kwa ine. Popeza anena za Inu moipa, ndi adani anu atchula dzina lanu mwachabe. Kodi sindidana nao iwo akudana ndi Inu, Yehova? Ndipo kodi sindimva nao chisoni iwo akuukira Inu? Ndidana nao ndi udani weniweni, ndiwayesa adani. Mundisanthule, Mulungu, nimudziwe mtima wanga; mundiyese nimudziwe zolingalira zanga. Ndipo mupenye ngati ndili nao mayendedwe oipa, nimunditsogolere pa njira yosatha. Kwa Mkulu wa Nyimbo; Salimo la Davide. Ndilanditseni, Yehova, kwa munthu woipa; ndisungeni kwa munthu wachiwawa; amene adzipanga zoipa mumtima mwao; masiku onse amemeza nkhondo. Anola lilime lao ngati njoka; pansi pa milomo yao pali ululu wa mphiri. Ndilindireni Yehova, ndisalowe m'manja mwa woipa; ndisungeni kwa munthu wachiwawa; kwa iwo akuti akankhe mapazi anga. Odzikuza ananditchera msampha, nandibisira zingwe; anatcha ukonde m'mphepete mwa njira; ananditchera makwekwe. Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga; munditcherere khutu mau a kupemba kwanga, Yehova. Yehova Ambuye, ndinu mphamvu ya chipulumutso changa, munandiphimba mutu wanga tsiku lakulimbana nkhondo. Yehova, musampatse woipa zokhumba iye; musamthandize zodzipanga zake; angadzikuze. Kunena za mutu wao wa iwo akundizinga, choipa cha milomo yao chiwaphimbe. Makala amoto awagwere; aponyedwe kumoto; m'maenje ozama, kuti asaukenso. Munthu wamlomo sadzakhazikika pa dziko lapansi; choipa chidzamsaka munthu wachiwawa kuti chimgwetse. Ndidziwa kuti Yehova adzanenera wozunzika mlandu, ndi kuweruzira aumphawi. Indedi, olungama adzayamika dzina lanu; oongoka mtima adzakhala pamaso panu. Salimo la Davide. Yehova, ndaitana kwa Inu; ndifulumireni ine; munditcherere khutu, pamene ndiitana kwa Inu. Pemphero langa liikike ngati chofukiza pamaso panu; kukweza manja anga kuikike ngati nsembe ya madzulo. Muike mdindo pakamwa panga, Yehova; sungani pakhomo pa milomo yanga. Mtima wanga usalinge kuchinthu choipa, kuchita ntchito zoipa ndi anthu akuchita zopanda pake; ndipo ndisadye zankhuli zao. Akandipanda munthu wolungama ndidzati nchifundo: akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu; mutu wanga usakane: Pakuti pangakhale posautsidwa iwo ndidzawapempherera. Oweruza ao anagwetseka pambali pa thanthwe; nadzamva mau anga kuti ndiwo okondweretsa. Mafupa athu amwazika pakamwa pa manda, monga ngati akumba nanyimphula nthaka yapansi. Pakuti maso anga apenya kwanu, Yehova Ambuye; ndithawira kwa Inu; musataye moyo wanga. Mundisunge ndisagwe mumsampha ananditcherawo, ndisakodwe m'makwekwe a iwo ochita zopanda pake. Oipa agwe pamodzi m'maukonde ao, kufikira nditapitirira ine. Chilangizo cha Davide, muja anakhala m'phanga; Pemphero. Ndifuula nalo liu langa kwa Yehova; ndi mau anga ndipemba kwa Yehova. Nditsanulira kudandaula kwanga pamaso pake; ndionetsa msauko wanga pamaso pake. Pamene mzimu wanga unakomoka m'kati mwanga, munadziwa njira yanga. M'njira ndiyendamo ananditchera msampha. Penyani kudzanja lamanja ndipo muone; palibe wondidziwa; pothawirapo pandisowa; palibe mmodzi wosamalira moyo wanga. Ndinafuulira kwa inu, Yehova; ndinati, Inu ndinu pothawirapo panga, gawo langa m'dziko la amoyo. Tamverani kufuula kwanga; popeza ndisauka kwambiri; ndilanditseni kwa iwo akundilondola; popeza andilaka. Tulutsani moyo wanga m'ndende, kuti ndiyamike dzina lanu; olungama adzandizinga; pakuti mudzandichitira zokoma. Salimo la Davide. Imvani pemphero langa, Yehova; nditcherere khutu kupemba kwanga; ndiyankheni mwa chikhulupiriko chanu, mwa chilungamo chanu. Ndipo musaitane mlandu wa mtumiki wanu; pakuti pamaso panu sipadzakhala wolungama wamoyo mmodzi yense. Pakuti mdani alondola moyo wanga; apondereza pansi moyo wanga; andikhalitsa mumdima monga iwo adafa kale lomwe. Potero mzimu wanga wakomoka mwa ine; mtima wanga utenga nkhawa m'kati mwanga. Ndikumbukira masiku a kale lomwe; zija mudazichita ndilingirirapo; ndikamba pandekha za ntchito ya manja anu. Nditambalitsira manja anga kwa Inu: Moyo wanga ulira Inu monga dziko lolira mvula. Fulumirani ndiyankheni, Yehova; mzimu wanga ukutha. Musandibisire nkhope yanu; ndingafanane nao akutsikira kudzenje. Mundimvetse chifundo chanu mamawa; popeza ndikhulupirira Inu: Mundidziwitse njira ndiyendemo; popeza ndikweza moyo wanga kwa Inu. Mundilanditse kwa adani anga, Yehova; ndibisala mwa Inu. Mundiphunzitse chokonda Inu; popeza Inu ndinu Mulungu wanga; Mzimu wanu ndi wokoma; munditsogolere kuchidikha. Mundipatse moyo, Yehova, chifukwa cha dzina lanu; mwa chilungamo chanu mutulutse moyo wanga m'sautso. Ndipo mwa chifundo chanu mundidulire adani anga, ndipo muononge onse akusautsa moyo wanga; pakuti ine ndine mtumiki wanu. Salimo la Davide. Wolemekezeka Yehova thanthwe langa, wakuphunzitsa manja anga achite nkhondo, zala zanga zigwirane nao: Ndiye chifundo changa, ndi linga langa, msanje wanga, ndi Mpulumutsi wanga; chikopa changa, ndi Iye amene ndimtama; amene andigonjetsera anthu anga. Yehova, munthu ndani kuti mumdziwa? Mwana wa munthu kuti mumsamalira? Munthu akunga mpweya; masiku ake akunga mthunzi wopitirira. Weramutsani thambo lanu, Yehova, nimutsike: Khudzani mapiri ndipo adzafuka. Ng'animitsani mphezi, ndi kuwabalalitsa; tumizani mivi yanu, ndi kuwapirikitsa. Tulutsani manja anu kuchokera m'mwamba; ndikwatuleni ndi kundilanditsa kumadzi aakulu, kudzanja la alendo; amene pakamwa pao alankhula zachabe, ndi dzanja lao lamanja ndilo dzanja lachinyengo. Ndidzakuimbirani nyimbo yatsopano, Mulungu; pa chisakasa cha zingwe khumi ndidzaimbira zakukulemekezani. Ndiye amene apatsa mafumu chipulumutso: Amene alanditsa Davide mtumiki wake kulupanga loipa. Ndilanditseni ndi kundipulumutsa kudzanja la alendo, amene pakamwa pao alankhula zachabe, ndi dzanja lao lamanja ndilo dzanja lachinyengo. Kuti ana athu amuna akhale ngati mmera udakula usanakhwime; ana athu akazi ngati nsanamira za kungodya, zosema zikometsere nyumba ya mfumu. Kuti nkhokwe zathu zidzale, kutipatsa za mitundumitundu; ndi kuti nkhosa zathu ziswane zikwizikwi, inde zikwi khumi kubusako. Kuti ng'ombe zathu zikhale zosenza katundu; ndi kuti pasakhale kupasula linga kapena kutulukamo, pasakhalenso kufuula m'makwalala athu. Odala anthu akuona zotere; odala anthu amene Mulungu wao ndi Yehova. Salimo lolemekeza; la Davide. Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu; ndipo ndidzalemekeza dzina lanu kunthawi za nthawi. Masiku onse ndidzakuyamikani; ndi kulemekeza dzina lanu kunthawi za nthawi. Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ndi ukulu wake ngwosasanthulika. Mbadwo wina udzalemekezera ntchito zanu mbadwo unzake, ndipo udzalalikira zamphamvu zanu. Ndidzalingalira ulemerero waukulu wa ulemu wanu, ndi ntchito zanu zodabwitsa. Ndipo adzanenera mphamvu za ntchito zanu zoopsa; ndi ukulu wanu ndidzaufotokozera. Adzabukitsa chikumbukiro cha ubwino wanu waukulu, nadzaimbira chilungamo chanu. Yehova ndiye wachisomo, ndi wachifundo; osakwiya msanga, ndi wa chifundo chachikulu. Yehova achitira chokoma onse; ndi nsoni zokoma zake zigwera ntchito zake zonse. Ntchito zanu zonse zidzakuyamikani, Yehova; ndi okondedwa anu adzakulemekezani. Adzanenera ulemerero wa ufumu wanu, adzalankhulira mphamvu yanu. Kudziwitsa ana a anthu zamphamvu zake, ndi ulemerero waukulu wa ufumu wake. Ufumu wanu ndiwo ufumu womka muyaya, ndi kuweruza kwanu kufikira mibadwo yonseyonse. Yehova agwiriziza onse akugwa, naongoletsa onse owerama. Maso a onse ayembekeza Inu; ndipo muwapatsa chakudya chao m'nyengo zao. Muolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chao. Yehova ali wolungama m'njira zake zonse, ndi wachifundo m'ntchito zake zonse. Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye, onse akuitanira kwa Iye m'choonadi. Adzachita chokhumba iwo akumuopa; nadzamva kufuula kwao, nadzawapulumutsa. Yehova asunga onse akukondana naye; koma oipa onse adzawaononga. Pakamwa panga padzanena chilemekezo cha Yehova; ndi zinthu zonse zilemekeze dzina lake loyera kunthawi za nthawi. Aleluya; Ulemekeze Yehova, moyo wanga. Ndidzalemekeza Yehova m'moyo mwanga; ndidzaimbira zomlemekeza Mulungu wanga pokhala ndi moyo ine. Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye. Mpweya wake uchoka, abwerera kunka kunthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika. Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti amthandize, chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake. Amene analenga zakumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zili m'mwemo. Ndiye wakusunga choonadi kosatha, ndiye wakuchitira chiweruzo osautsika; ndiye wakupatsa anjala chakudya; Yehova amasula akaidi. Yehova apenyetsa osaona; Yehova aongoletsa onse owerama; Yehova akonda olungama. Yehova asunga alendo; agwiriziza mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye; koma akhotetsa njira ya oipa. Yehova adzachita ufumu kosatha, Mulungu wako, Ziyoni, ku mibadwomibadwo. Aleluya. Aleluya; Pakuti kuimbira zomlemekeza Mulungu wathu nkokoma; pakuti chikondwetsa ichi, chilemekezo chiyenera. Yehova amanga Yerusalemu; asokolotsa otayika a Israele. Achiritsa osweka mtima, namanga mabala ao. Awerenga nyenyezi momwe zili; azitcha maina zonsezi. Ambuye wathu ndi wamkulu ndi wa mphamvu zambiri; nzeru yake njosatha. Yehova agwiriziza ofatsa; atsitsira oipa pansi. Yamikani Yehova ndi kuthira mang'ombe; muimbireni Mulungu wathu zomlemekeza pazeze: Amene aphimba thambo ndi mitambo, amene akonzera mvula nthaka, amene aphukitsa msipu pamapiri. Amene apatsa zoweta chakudya chao, ana a khungubwi alikulira. Mphamvu ya kavalo siimkonda: Sakondwera nayo miyendo ya munthu. Yehova akondwera nao akumuopa Iye, iwo akuyembekeza chifundo chake. Yerusalemu, lemekezani Yehova; Ziyoni, lemekezani Mulungu wanu. Popeza analimbitsa mipiringidzo ya zitseko zanu: Anadalitsa ana anu m'kati mwanu. Ndiye amene akhalitsa malire anu mumtendere; akukhutitsani ndi tirigu wakucha bwino. Atumiza lamulo lake kudziko lapansi; mau ake athamanga liwiro. Apatsa chipale chofewa ngati ubweya; awaza chisanu ngati phulusa. Aponya matalala ake ngati zidutsu: Adzaima ndani pa kuzizira kwake? Atumiza mau ake nazisungunula; aombetsa mphepo yake, ayenda madzi ake. Aonetsa mau ake kwa Yakobo; malemba ake, ndi maweruzo ake kwa Israele. Sanatero nao anthu a mtundu wina; ndipo za maweruzo ake, sanawadziwe. Aleluya. Aleluya. Lemekezani Yehova kochokera kumwamba; mlemekezeni m'misanje. Mlemekezeni, angelo ake onse; mlemekezeni, makamu ake onse. Mlemekezeni, dzuwa ndi mwezi; mlemekezeni, nyenyezi zonse zounikira. Mlemekezeni, m'mwambamwamba, ndi madzi inu, a pamwamba pa thambo. Alemekeze dzina la Yehova; popeza analamulira, ndipo zinalengedwa. Anazikhazikanso kunthawi za nthawi; anazipatsa chilamulo chosatumphika. Lemekezani Yehova kochokera ku dziko lapansi, zinsomba inu, ndi malo ozama onse; moto ndi matalala, chipale chofewa ndi nkhungu; mphepo ya namondwe, yakuchita mau ake; mapiri ndi zitunda zonse; mitengo yazipatso ndi yamikungudza yonse: Nyama za kuthengo ndi zoweta zonse; zokwawa, ndi mbalame zakuuluka. Mafumu a padziko ndi mitundu yonse ya anthu; zinduna ndi oweruza onse a padziko. Anyamata ndiponso anamwali; okalamba pamodzi ndi ana. Alemekeze dzina la Yehova; pakuti dzina lake lokha ndi lokwezeka; ulemerero wake uli pamwamba pa dziko lapansi ndi thambo. Ndipo anakweza nyanga ya anthu ake, chilemekezo cha okondedwa ake onse; ndiwo ana a Israele, anthu a pafupi pa Iye. Aleluya. Aleluya, Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano, ndi chilemekezo chake mu msonkhano wa okondedwa ake. Akondwere Israele mwa Iye amene anamlenga; ana a Ziyoni asekere mwa mfumu yao. Alemekeze dzina lake ndi kuthira mang'ombe; amuimbire zomlemekeza ndi lingaka ndi zeze. Popeza Yehova akondwera nao anthu ake; adzakometsa ofatsa ndi chipulumutso. Okondedwa ake atumphe mokondwera m'ulemu: Afuule mokondwera pamakama pao. Nyimbo zakukweza Mulungu zikhale pakamwa pao, ndi lupanga lakuthwa konsekonse m'dzanja lao; kubwezera chilango akunja, ndi kulanga mitundu ya anthu; kumanga mafumu ao ndi maunyolo, ndi omveka ao ndi majerejede achitsulo, kuwachitira chiweruzo cholembedwacho. Ulemu wa okondedwa ake onse ndi uwu. Aleluya. Aleluya. Lemekezani Mulungu m'malo ake oyera; mlemekezeni m'thambo la mphamvu yake. Mlemekezeni chifukwa cha ntchito zake zolimba; mlemekezeni monga mwa ukulu wake waunjinji. Mlemekezeni ndi kulira kwa lipenga; mlemekezeni ndi chisakasa ndi zeze. Mlemekezeni ndi lingaka ndi kuthira mang'ombe: Mlemekezeni ndi zoimbira za zingwe ndi chitoliro. Mlemekezeni ndi nsanje zomveka: Mlemekezeni ndi nsanje zoliritsa. Zonse zakupuma zilemekeze Yehova. Aleluya. Miyambo ya Solomoni mwana wa Davide, mfumu ya Israele. Kudziwa nzeru ndi mwambo; kuzindikira mau ozindikiritsa; kulandira mwambo wakusamalira machitidwe, chilungamo, chiweruzo ndi zolunjika; kuchenjeza achibwana, kuphunzitsa mnyamata kudziwa ndi kulingalira; kuti wanzeru amve, naonjezere kuphunzira; ndi kuti wozindikira afikire kuuphungu; kuzindikira mwambi ndi tanthauzo lake, mau a anzeru, ndi zophiphiritsa zao. Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha kudziwa; opusa anyoza nzeru ndi mwambo. Mwananga, tamva mwambo wa atate wako, ndi kusasiya chilangizo cha amai ako; pakuti izi ndi korona wa chisomo pamtu pako, ndi mkanda pakhosi pako. Mwananga, akakukopa ochimwa usalole. Akanena, Idza nafe, tibisalire mwazi, tilalire osachimwa opanda chifukwa; tiwameze ali ndi moyo ngati manda, ali amphumphu, ngati akutsikira kudzenje; tidzapeza chuma chonse cha mtengo wake, tidzadzaza nyumba zathu ndi zofunkha; udzachita nafe maere, tonse tidzakhala ndi chotengeramo chimodzi. Mwananga, usayende nao m'njira; letsa phazi lako ku mayendedwe ao; pakuti mapazi ao athamangira zoipa, afulumira kukhetsa mwazi. Pakuti kutchera msampha pamaso pa mbalame ndi chabe; ndipo awa abisalira mwazi waowao, alalira miyoyo yaoyao. Mayendedwe a yense wopindula chuma monyenga ngotere; chilanda moyo wa eni ake. Nzeru ifuula panja; imveketsa mau ake pabwalo; iitana posonkhana anthu polowera pachipata; m'mudzi inena mau ake, Kodi mudzakonda zazibwana kufikira liti, achibwana inu? Onyoza ndi kukonda kunyoza, opusa ndi kuda nzeru? Tembenukani pamene ndikudzudzulani; taonani, nditsanulira pa inu mzimu wanga, ndikudziwitsani mau anga. Chifukwa ndaitana, ndipo munakana; ndatambasula dzanja langa, ndipo panalibe analabadira; koma munapeputsa uphungu wanga wonse, ndi kukana kudzudzula kwanga. Inetu ndidzachitira chiphwete tsoka lanu, ndidzatonyola pakudza mantha anu; pakudza mantha anu ngati mphepo yopasula, ndi pofika tsoka lanu ngati kamvulumvulu; pakudza kwa inu vuto ndi nsautso. Pamenepo adzandiitana, koma sindidzavomera; adzandifunatu, osandipeza ai; chifukwa anada nzeru, sanafune kuopa Yehova; anakana uphungu wanga, nanyoza kudzudzula kwanga konse; momwemo adzadya zipatso za mayendedwe ao, nadzakhuta zolingalira zao. Pakuti kubwerera m'mbuyo kwa achibwana kudzawapha; ndipo mphwai za opusa zidzawaononga. Koma wondimvera ine adzakhala osatekeseka, nadzakhala phee osaopa zoipa. Mwananga, ukalandira mau anga, ndi kusunga malamulo anga; kutcherera makutu ako kunzeru, kulozetsa mtima wako kukuzindikira; ukaitananso luntha, ndi kufuulira kuti ukazindikire; ukaifunafuna ngati siliva, ndi kuipwaira ngati chuma chobisika; pompo udzazindikira kuopa Yehova ndi kumdziwadi Mulungu. Pakuti Yehova apatsa nzeru; kudziwa ndi kuzindikira kutuluka m'kamwa mwake. Iye asungira oongoka mtima nzeru yeniyeni; ndiye chikopa cha oyenda molunjika; kuti atchinjirize njira za chiweruzo, nadikire khwalala la opatulidwa ake. Pamenepo udzazindikira chilungamo ndi chiweruzo, zolunjika ndi mayendedwe onse abwino. Pakuti nzeru idzalowa m'mtima mwako, moyo wako udzakondwera ndi kudziwa, kulingalira kudzakudikira, kuzindikira kudzakutchinjiriza; kukupulumutsa kunjira yoipa, kwa anthu onena zokhota; akusiya mayendedwe olungama, akayende m'njira za mdima; omwe asangalala pochita zoipa, nakondwera ndi zokhota zoipa; amene apotoza njira zao, nakhotetsa mayendedwe ao. Nzeru idzakupulumutsa kwa mkazi wachiwerewere, kwa mkazi wachilendo wosyasyalika ndi mau ake; wosiya bwenzi la ubwana wake, naiwala chipangano cha Mulungu wake. Nyumba yake itsikira kuimfa, ndi mayendedwe ake kwa akufa; onse akunka kwa iye sabweranso, safika kunjira za moyo; nzeru idzakuyendetsa m'njira ya anthu abwino, kuti usunge mayendedwe a olungama. Pakuti oongoka mtima adzakhala m'dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m'dziko, achiwembu adzazulidwamo. Mwananga, usaiwale malamulo anga, mtima wako usunge malangizo anga; pakuti adzakuonjezera masiku ambiri, ndi zaka za moyo ndi mtendere. Chifundo ndi choonadi zisakusiye; uzimange pakhosi pako; uzilembe pamtima pako; motero udzapeza chisomo ndi nzeru yabwino, pamaso pa Mulungu ndi anthu. Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako. Usadziyese wekha wanzeru; opa Yehova, nupatuke pazoipa; mitsempha yako idzalandirapo moyo, ndi mafupa ako uwisi. Lemekeza Yehova ndi chuma chako, ndi zinthu zako zonse zoyambirira kucha; motero nkhokwe zako zidzangoti thee, mbiya zako zidzasefuka vinyo. Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova, ngakhale kutopa ndi kudzudzula kwake; pakuti Yehova adzudzula omwe awakonda; monga atate mwana amene akondwera naye. Wodala ndi wopeza nzeru, ndi woona luntha; pakuti malonda a nzeru aposa malonda a siliva, phindu lake liposa golide woyengeka. Mtengo wake uposa ngale; ndipo zonse zikukondweretsa sizilingana naye. Masiku ambiri ali m'dzanja lamanja lake; chuma ndi ulemu m'dzanja lake lamanzere. Njira zake zili zokondweretsa, mayendedwe ake onse ndiwo mtendere. Ndiyo mtengo wa moyo wa akuigwira; wakuiumirira ngwodala. Yehova anakhazika dziko ndi nzeru; naika zamwamba ndi luntha. Zakuya zinang'ambika ndi kudziwa kwake; thambo ligwetsa mame. Mwananga, zisachokere kumaso ako; sunga nzeru yeniyeni ndi kulingalira; ndipo mtima wako udzatengapo moyo, ndi khosi lako chisomo. Pompo udzayenda m'njira yako osaopa, osaphunthwa phazi lako. Ukagona, sudzachita mantha; udzagona tulo tokondweretsa. Usaope zoopsa zodzidzimutsa, ngakhale zikadza zopasula oipa; pakuti Yehova adzalimbitsa mtima wako, nadzasunga phazi lako lingakodwe. Oyenera kulandira zabwino usawamane; pokhoza dzanja lako kuwachitira zabwino. Usanene kwa mnzako, Ukabwerenso, ndipo mawa ndidzakupatsa; pokhala uli nako kanthu. Usapangire mnzako chiwembu; popeza akhala nawe pafupi osatekeseka. Usakangane ndi munthu chabe, ngati sanakuchitire choipa. Usachitire nsanje munthu wachiwawa; usasankhe njira yake iliyonse. Pakuti wamphulupulu anyansa Yehova; koma chinsinsi chake chili ndi oongoka. Yehova atemberera za m'nyumba ya woipa; koma adalitsa mokhalamo olungama. Anyozadi akunyoza, koma apatsa akufatsa chisomo. Anzeru adzalandira ulemu cholowa chao; koma opusa adzakweza manyazi. Ananu, mverani mwambo wa atate, nimutchere makutu mukadziwe luntha; pakuti ndikuphunzitsani zabwino; musasiye chilangizo changa. Pakuti ndinali mwana kwa atate wanga, wokondedwa ndi mai, ndine ndekha, sanabale wina. Atate nandiphunzitsa, nati kwa ine, mtima wako uumirire mau anga; sunga malamulo anga, nukhale ndi moyo. Tenga nzeru, tenga luntha; usaiwale, usapatuke pa mau a m'kamwa mwanga; usasiye nzeru, ndipo idzakusunga; uikonde, idzakutchinjiriza. Nzeru ipambana, tatenga nzeru; m'kutenga kwako konseko utenge luntha. Uilemekeze, ndipo idzakukweza; idzakutengera ulemu pamene uifungatira. Idzaika chisada cha chisomo pamtu pako; idzakupatsa korona wokongola. Tamvera mwananga, nulandire mau anga; ndipo zaka za moyo wako zidzachuluka. Ndakuphunzitsa m'njira ya nzeru, ndakuyendetsa m'mayendedwe olungama. Mapazi ako sadzaombana ulikuyenda; ukathamanga, sudzaphunthwa. Gwira mwambo, osauleka; uusunge; pakuti ndiwo moyo wako. Usalowe m'mayendedwe ochimwa, usayende m'njira ya oipa. Pewapo, osapitamo; patukapo, nupitirire. Pakuti akapanda kuchita zoipa, samagona; ndipo akapanda kukhumudwitsa wina, tulo tao tiwachokera. Pakuti amadya chakudya cha uchimo, namwa vinyo wa chifwamba. Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha, kunkabe kuwala kufikira usana woti mbee. Njira ya oipa ikunga mdima; sadziwa chimene chiwaphunthwitsa. Mwananga, tamvera mau anga; tcherera makutu ku zonena zanga. Asachoke kumaso ako; uwasunge m'kati mwa mtima wako. Pakuti ali moyo kwa omwe awapeza, nalamitsa thupi lao lonse. Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo. Tasiya m'kamwa mokhota, uike patali milomo yopotoka. Maso ako ayang'ane m'tsogolo, zikope zako zipenye moongoka. Sinkasinkha bwino mayendedwe a mapazi ako; njira zako zonse zikonzeke. Usapatuke kudzanja lamanja kapena kulamanzere; suntha phazi lako kusiya zoipa. Mwananga, mvera nzeru yanga; tcherera makutu ku luntha langa; ukasunge zolingalira, milomo yako ilabadire zomwe udziwa. Pakuti milomo ya mkazi wachiwerewere ikukha uchi; m'kamwa mwake muti see koposa mafuta. Chimaliziro chake nchowawa ngati chivumulo, ndi chakuthwa ngati lupanga lakuthawa konsekonse. Mayendedwe ake atsikira kuimfa; mapazi ake aumirira kumanda; sasinkhasinkha bwino za njira ya moyo; mayendedwe ake adzandira dzandidzandi osadziwa iye. Ndipo tsopano ana, mundimvere, musapatuke ku mau a m'kamwa mwanga. Siyanitsa njira yako kutali kwa iyeyo, osayandikira ku khomo la nyumba yake; kuti ungapereke ulemu wako kwa ena, ndi zaka zako kwa ankhanza; kuti mphamvu yako isakhutitse alendo, ndi kuti usagwire ntchito m'nyumba ya wachilendo; ungalire pa chimaliziro chako, pothera nyama yako ndi thupi lako; ndi kuti, Bwanji ndinada mwambo, mtima wanga ndi kunyoza chidzudzulo; ndipo sindinamvera mau a aphunzitsi anga; ngakhale kutcherera makutu kwa akundilanga mwambo! Ndikadakhala m'zoipa zonse, m'kati mwa msonkhano ndi khamu la anthu. Imwa madzi a m'chitsime mwako, ndi madzi oyenda a m'kasupe mwako. Kodi magwero ako ayenera kumwazika kunja, ndi mitsinje ya madzi m'makwalala? Ikhale ya iwe wekha, si ya alendo okhala nawe ai. Adalitsike kasupe wako; ukondwere ndi mkazi wokula nayo. Ngati mbawala yokonda ndi chinkhoma chachisomo, maere ake akukwanire nthawi zonse; ukodwe ndi chikondi chake osaleka. Pakuti ukondwerenji, mwananga, ndi mkazi wachiwerewere, ndi kufungatira chifuwa cha mkazi wachilendo? Pakuti njira za munthu zili pamaso pa Yehova, asinkhasinkha za mayendedwe ake onse. Zoipa zakezake zidzagwira woipa; adzamangidwa ndi zingwe za uchimo wake. Adzafa posowa mwambo; adzasochera popusa kwambiri. Mwananga, ngati waperekera mnzako chikole, ngati wapangana kulipirira mlendo, wakodwa ndi mau a m'kamwa mwako, wagwidwa ndi mau a m'kamwa mwako. Chita ichi tsono; mwananga, nudzipulumutse; popeza walowa m'dzanja la mnzako, pita nudzichepetse, numdandaulire mnzako. Usaone tulo m'maso mwako, ngakhale kuodzera zikope zako. Dzipulumutse wekha ngati mphoyo kudzanja la msaki, ndi mbalame kudzanja la msodzi. Pita kunyerere, waulesi iwe, penya njira zao nuchenjere; zilibe mfumu, ngakhale kapitao, ngakhale mkulu; koma zitengeratu zakudya zao m'malimwe; nizituta dzinthu zao m'masika. Udzagona mpaka liti, waulesi iwe? Udzauka kutulo tako liti? Tulo ta pang'ono, kuodzera pang'ono, kungomanga manja pang'ono, ndi kugona; ndipo umphawi wako udzafika ngati mbala, ndi kusauka kwako ngati munthu wachikopa. Munthu wopanda pake, mwamuna wamphulupulu; amayenda ndi m'kamwa mokhota. Amatsinzinira ndi maso ake, napalasira ndi mapazi ake, amalankhula ndi zala zake; zopotoka zili m'mtima mwake, amaganizira zoipa osaleka; amapikisanitsa anthu. Chifukwa chake tsoka lake lidzadza modzidzimuka; adzasweka msangamsanga, palibe chompulumutsa. Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi Yehova azida; ngakhale zisanu ndi ziwiri zimnyansa: Maso akunyada, lilime lonama, ndi manja akupha anthu osachimwa; mtima woganizira ziwembu zoipa, mapazi akuthamangira mphulupulu m'mangum'mangu; mboni yonama yonong'ona mabodza, ndi wopikisanitsa abale. Mwananga, sunga malangizo a atate wako, usasiye malamulo a mai ako; uwamange pamtima pako osaleka; uwalunze pakhosi pako. Adzakutsogolera ulikuyenda, ndi kukudikira uli m'tulo, ndi kulankhula nawe utauka. Pakuti malangizo ndi nyali, malamulo ndi kuunika; ndi zidzudzulo za mwambo ndizo njira ya moyo. Zikutchinjiriza kwa mkazi woipa, ndi kulilime losyasyalika la mkazi wachiwerewere. Asakuchititse kaso m'mtima mwako, asakukole ndi zikope zake. Pakuti ukayamba ndi mkazi wadama, udzamaliza ndi nyenyeswa; ndipo mkazi wa mwini amasaka moyo wa mtengo wapatali. Kodi mwamuna angatenge moto pa chifuwa chake, osatentha zovala zake? Pena kodi mwamuna angayende pa makala oyaka, osapsa mapazi ake? Chomwecho wolowa kwa mkazi wa mnzake; womkhudzayo sadzapulumuka chilango. Anthu sanyoza mbala ikaba, kuti ikhutitse mtima wake pomva njala; koma ikapezedwa idzabwezera kasanu ndi kawiri; idzapereka chuma chonse cha m'nyumba yake. Wochita chigololo ndi mkazi alibe nzeru; wofuna kuononga moyo wakewake ndiye amatero. Adzalasidwa nanyozedwa; chitonzo chake sichidzafafanizidwa. Pakuti nsanje ndiyo ukali wa mwamuna, ndipo sadzachitira chifundo tsiku lobwezera chilango. Sadzalabadira chiombolo chilichonse, sadzapembedzeka ngakhale uchulukitsa malipo. Mwananga, sunga mau anga, ukundike malangizo anga, Sunga malangizo anga, nukhale ndi moyo; ndi malamulo anga ngati mwana wa diso lako. Uwamange pa zala zako, uwalembe pamtima pako. Nena kwa nzeru, Ndiwe mlongo wanga; nutche luntha mbale wako. Kuti zikutchinjirizire kwa mkazi wachiwerewere, kwa mlendo wamkazi wosyasyalika ndi mau ake. Pakuti pa zenera la nyumba yanga ndinapenyera pamwamba pake; ndinaona pakati pa achibwana, ndinazindikira pakati pa ang'ono mnyamata wopanda nzeru, alikupita pakhwalala pafupi ndi mphambano ya pa mkaziyo, ndi kuyenda pa njira ya kunyumba yake; pa madzulo kuli sisiro, pakati pa usiku pali mdima. Ndipo taona, mkaziyo anamchingamira, atavala zadama wochenjera mtima, ali wolongolola ndi wosaweruzika, mapazi ake samakhala m'nyumba mwake. Mwina ali kumakwalala, mwina ali kumabwalo, nabisalira pa mphambano zonse. Ndipo anagwira mnyamatayo, nampsompsona; nati kwa iye ndi nkhope yachipongwe, nsembe zamtendere zili nane; lero ndachita zowinda zanga. Chifukwa chake ndatuluka kudzakuchingamira, kudzafunitsa nkhope yako, ndipo ndakupeza. Ndayala zofunda pakama panga, nsalu zamawangamawanga za thonje la ku Ejipito, ndakapiza pamphasa panga mankhwala onunkhira a mure ndi chisiyo ndi sinamoni. Tiye tikondwere ndi chikondano mpaka mamawa; tidzisangalatse ndi chiyanjano. Pakuti mwamuna kulibe kwathu, wapita ulendo wa kutali; watenga thumba la ndalama m'dzanja lake, tsiku lowala mwezi adzabwera kwathu. Amkakamiza ndi kukoka kwa mau ake, ampatutsa ndi kusyasyalika kwa milomo yake. Mnyamatayo amtsata posachedwa, monga ng'ombe ipita kukaphedwa; ndi monga unyolo umadza kulanga chitsiru; mpaka muvi ukapyoza mphafa yake; amtsata monga mbalame yothamangira msampha; osadziwa kuti adzaononga moyo wake. Ndipo tsopano, ananga, mundimvere ine, labadirani mau a m'kamwa mwanga. Mtima wako usapatukire kunjira ya mkaziyo, usasochere m'mayendedwe ake. Pakuti amagwetsa ambiri, atawalasa; ndipo ophedwa ndi iye achulukadi. Nyumba yake ndiyo njira ya kumanda, yotsikira kuzipinda za imfa. Kodi nzeru siitana, luntha ndi kukweza mau ake? Iima pamwamba pa mtunda, pa mphambano za makwalala; pambali pa chipata polowera m'mudzi, polowa anthu pa makomo ifuula: Ndinu ndikuitanani, amuna, mau anga ndilankhula kwa ana a anthu. Achibwana inu, chenjerani, opusa inu, khalani ndi mtima wozindikira; imvani, pakuti ndikanena zoposa, ndi zolungama potsegula pakamwa panga. Pakuti m'kamwa mwanga mudzalankhula ntheradi, zoipa zinyansa milomo yanga. Mau onse a m'kamwa mwanga alungama; mwa iwo mulibe zokhota ndi zopotoka. Onsewo amveka ndi iye amene azindikira; alungama kwa akupeza nzeru. Landirani mwambo wanga, si siliva ai; ndi nzeru kopambana ndi golide wosankhika. Pakuti nzeru iposa ngale, ndi zonse tizifunitsa sizilingana nayo. Ine Nzeru ndikhala m'kuchenjera, ngati m'nyumba yanga; ndimapeza kudziwa ndi zolingalira. Kuopa Yehova ndiko kuda zoipa; kunyada, ndi kudzikuza, ndi njira yoipa, ndi m'kamwa mokhota, ndizida. Ndine mwini uphungu ndi kudziwitsa; ndine luntha; ndili ndi mphamvu. Mwa ine mafumu alamulira; akazembe naweruza molungama. Mwa ine akalonga ayang'anira, ndi akulu, ngakhale oweruza onse a m'dziko. Akundikonda ndiwakonda; akundifunafuna adzandipeza. Katundu ndi ulemu zili ndi ine, chuma chosatha ndi chilungamo. Chipatso changa chiposa golide, ngakhale golide woyengeka; phindu langa liposa siliva wosankhika. Ndimayenda m'njira ya chilungamo, pakati pa mayendedwe a chiweruzo, kuti ndionetse chuma akundikonda, chikhale cholowa chao, ndi kudzaza mosungira mwao. Yehova anali nane poyamba njira yake, asanalenge zake zakale. Anandiimika chikhalire chiyambire, dziko lisanalengedwe. Pamene panalibe zozama ndinabadwa ine, pamene panalibe akasupe odzala madzi. Mapiri asanakhazikike, zitunda zisanapangidwe, ndinabadwa. Asanalenge dziko, ndi thengo, ngakhale chiyambi cha fumbi la dziko. Pamene anakhazika mlengalenga ndinali pompo; pamene analemba pazozama kwetekwete; polimbitsa Iye thambo la kumwamba, pokula akasupe a zozama. Poikira nyanja malire ake, kuti madzi asapitirire pa lamulo lake; polemba maziko a dziko. Ndinali pa mbali pake ngati mmisiri; ndinamsekeretsa tsiku ndi tsiku, ndi kukondwera pamaso pake nthawi zonse; ndi kukondwera ndi dziko lake lokhalamo anthu, ndi kusekerera ndi ana a anthu. Ndipo tsopano, ananga, mundimvere ine, ngodala akusunga njira zanga. Imvani mwambo, mukhale anzeru osaukana. Ngwodala amene andimvera, nadikira pa zitseko zanga tsiku ndi tsiku, ndi kulinda pa mphuthu za makoma anga; pakuti wondipeza ine apeza moyo; Yehova adzamkomera mtima. Koma wondichimwira apweteka moyo wake; onse akundida ine akonda imfa. Nzeru yamanga nyumba yake, yasema zoimiritsa zake zisanu ndi ziwiri; yaphera nyama yake, nisanganiza vinyo wake, nilongosolanso pa gome lake. Yatuma anamwali ake, iitana pa misanje ya m'mudzi. Wazibwana yense apatukire kuno; iti kwa yense wosowa nzeru, Tiyeni, idyani chakudya changa; nimumwe vinyo wanga ndamsanganiza. Lekani, achibwana inu, nimukhale ndi moyo; nimuyende m'njira ya nzeru. Woweruza munthu wonyoza adzichititsa yekha manyazi; yemwe adzudzula wochimwa angodetsa mbiri yakeyake. Usadzudzule wonyoza kuti angakude; dzudzula wanzeru adzakukonda. Ukachenjeza wanzeru adzakulitsa nzeru yake; ukaphunzitsa wolungama adzaonjezera kuphunzira. Chiyambi cha nzeru ndicho kuopa Yehova; kudziwa Woyerayo ndiko luntha. Pakuti mwa ine masiku ako adzachuluka, zaka za moyo wako zidzaonjezedwa. Ukakhala wanzeru, si yakoyako nzeruyo? Ndipo ukanyoza udzasauka wekha. Utsiru umalongolola, ngwa chibwana osadziwa kanthu. Ukhala pa khomo la nyumba yake, pampando pa misanje ya m'mudzi, kuti uitane akupita panjira, amene angonkabe m'kuyenda kwao, wachibwana ndani? Apatukire kuno. Ati kwa yense wopanda nzeru, madzi akuba atsekemera, ndi chakudya chobisika chikoma. Ndipo mwamunayo sadziwa kuti akufa ali konko; omwe achezetsa utsiru ali m'manda akuya. Miyambo ya Solomoni: Mwana wanzeru akondweretsa atate; koma mwana wopusa amvetsa amake chisoni. Chuma cha uchimo sichithangata; koma chilungamo chipulumutsa kuimfa. Yehova samvetsa njala moyo wa wolungama; koma amainga chifuniro cha wochimwa. Wochita ndi dzanja laulesi amasauka; koma dzanja la akhama lilemeretsa. Wokolola m'malimwe ndi mwana wanzeru; koma wogona pakutula ndi mwana wochititsa manyazi. Madalitso ali pamtu pa wolungama; koma m'kamwa mwa oipa mubisa chiwawa. Amayesa wolungama wodala pomkumbukira; koma dzina la oipa lidzavunda. Mwini mtima wanzeru amalandira malamulo; koma chitsiru cholongolola chidzagwa. Woyenda moongoka amayenda osatekeseka; koma wokhotetsa njira zake adzadziwika. Wotsinzinira achititsa chisoni; koma wodzudzula momveka achita mtendere. M'kamwa mwa wolungama ndi kasupe wa moyo; koma m'kamwa mwa oipa mubisa chiwawa. Udani upikisanitsa; koma chikondi chikwirira zolakwa zonse. Nzeru ipezedwa m'milomo ya wozindikira; koma wopusa pamsana pake nthyole. Anzeru akundika zomwe adziwa; koma m'kamwa mwa chitsiru muononga tsopano lino. Chuma cha wolemera ndi mudzi wake wolimba; koma umphawi wao uononga osauka. Ntchito za wolungama zipatsa moyo; koma phindu la oipa lichimwitsa. Wosunga mwambo ali m'njira ya moyo; koma wosiya chidzudzulo asochera. Wobisa udani ali ndi milomo yonama; wonena ugogodi ndiye chitsiru. Pochuluka mau zolakwa sizisoweka; koma wokhala chete achita mwanzeru. Lilime la wolungama likunga siliva wosankhika; koma mtima wa oipa uli wachabe. Milomo ya wolungama imadyetsa ambiri; koma zitsiru zimafa posowa nzeru. Madalitso a Yehova alemeretsa, saonjezerapo chisoni. Masewero a chitsiru ndiwo kuchita zoipa; koma masewero a wozindikira ndiwo nzeru. Chomwe woipa achiopa chidzamfikira; koma chomwe olungama achifuna chidzapatsidwa. Monga kavumbulu angopita, momwemo woipa kuli zii; koma olungama ndiwo maziko osatha. Ngati vinyo wowawa m'mano, ndi utsi m'maso, momwemo waulesi kwa iwo amene amtuma. Kuopa Yehova kutanimphitsa masiku; koma zaka za oipa zidzafinimpha. Chiyembekezo cha olungama ndicho chimwemwe; koma chidikiro cha oipa chidzaonongeka. Njira ya Yehova ndi linga kwa woongoka mtima; koma akuchita zoipa adzaonongeka. Wolungama sadzachotsedwa konse; koma oipa sadzakhalabe m'dziko. M'kamwa mwa wolungama mulankhula nzeru; koma lilime lokhota lidzadulidwa. Milomo ya wolungama idziwa zokondweretsa; koma m'kamwa mwa oipa munena zokhota. Muyeso wonyenga unyansa Yehova; koma mulingo wamphumphu umsekeretsa. Pakudza kudzikuza padzanso manyazi; koma nzeru ili ndi odzichepetsa. Kuongoka mtima kwa olungama kuwatsogolera; koma kukhota kwa achiwembu kudzawaononga. Chuma sichithandiza tsiku la mkwiyo; koma chilungamo chipulumutsa kuimfa. Chilungamo cha wangwiro chimaongola njira yake; koma woipa adzagwa ndi zoipa zake. Chilungamo cha oongoka mtima chidzawapulumutsa; koma achiwembu adzagwidwa ndi mphulupulu yao. Pomwalira woipa chidikiro chake chionongeka; chiyembekezo cha uchimo chionongeka. Wolungama apulumuka kuvuto; woipa nalowa m'malo mwake. Wonyoza Mulungu aononga mnzake ndi m'kamwa mwake; koma olungama adzapulumuka pakudziwa. Olungama akapeza bwino, mudzi usekera; nufuula pakuonongeka oipa. Madalitso a olungama akuza mudzi; koma m'kamwa mwa oipa muupasula. Wopeputsa mnzake asowa nzeru; koma wozindikira amatonthola. Kazitape woyendayenda amawanditsa zinsinsi; koma wokhulupirika mtima abisa mau. Popanda upo wanzeru anthu amagwa; koma pochuluka aphungu pali chipulumutso. Woperekera mlendo chikole adzaphwetekwapo; koma wakuda chikole akhala ndi mtendere. Mkazi wodekha agwiritsa ulemu; aukali nagwiritsa chuma. Wachifundo achitira moyo wake zokoma; koma wankhanza avuta nyama yake. Woipa alandira malipiro onyenga; koma wofesa chilungamo aonadi mphotho. Wolimbikira chilungamo alandira moyo; koma wolondola zoipa adzipha yekha. Okhota mtima anyansa Yehova; koma angwiro m'njira zao amsekeretsa. Zoonadi, wochimwa sadzapulumuka chilango; koma mbeu ya olungama idzalanditsidwa. Monga chipini chagolide m'mphuno ya nkhumba, momwemo mkazi wokongola wosasinkhasinkha bwino. Chifuniro cha olungama chifikitsa zabwino zokha; koma chiyembekezo cha oipa mkwiyo. Alipo wogawira, nangolemerabe; aliponso womana chomwe ayenera kupatsa nangosauka. Mtima wa mataya udzalemera; wothirira madzi nayenso adzathiriridwa. Womana tirigu anthu amtemberera; koma madalitso adzakhala pamtu pa wogulitsa. Wopwaira ubwino afunitsa chikondwerero; koma zoipa zidzamfikira wozilondola. Wokhulupirira chuma chake adzagwa; koma olungama adzaphuka ngati tsamba. Wovuta banja lake adzalowa m'zomsautsa; wopusa adzatumikira wanzeru. Chipatso cha wolungama ndi mtengo wa moyo; ndipo wokola mtima ali wanzeru. Taonani, wolungama adzalandira mphotho kunja kuno; koposa kotani woipa ndi wochimwa? Wokonda mwambo akonda kudziwa; koma wakuda chidzudzulo apulukira. Yehova akomera mtima munthu wabwino; koma munthu wa ziwembu amtsutsa. Munthu sadzakhazikika ndi udyo, muzu wa olungama sudzasunthidwa. Mkazi wodekha ndiye korona wa mwamuna wake; koma wochititsa manyazi akunga chovunditsa mafupa a mwamunayo. Maganizo a olungama ndi chiweruzo; koma uphungu wa oipa unyenga. Mau a oipa abisalira mwazi; koma m'kamwa mwa olungama muwalanditsa. Oipa amagwa kuli zii; koma banja la olungama limaimabe. Munthu amatamandidwa monga mwa nzeru yake; koma wokhota mtima adzanyozedwa. Wonyozedwa, amene ali ndi kapolo, aposa wodzikuza, amene asowa zakudya. Wolungama asamalira moyo wa choweta chake; koma chifundo cha oipa ndi nkhanza. Zakudya zikwanira wolima minda yake; koma wotsata anthu opanda pake asowa nzeru. Woipa akhumba chokodwa ndi amphulupulu; koma muzu wa olungama umabala zipatso. M'kulakwa kwa milomo muli msampha woipa; koma wolungama amatuluka m'mavuto. Munthu amakhuta zabwino ndi zipatso za m'kamwa mwake; zochita za manja ake zidzabwezedwa kwa iye. Njira ya chitsiru njolungama pamaso pakepake; koma wanzeru amamvera uphungu. Mkwiyo wa chitsiru udziwika posachedwa; koma wanzeru amabisa manyazi. Wolankhula ntheradi aonetsa chilungamo; koma mboni yonama imanyenga. Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga; koma lilime la anzeru lilamitsa. Mlomo wa ntheradi ukhazikika nthawi zonse; koma lilime lonama likhala kamphindi. Chinyengo chili m'mitima ya oganizira zoipa; koma aphungu a mtendere amakondwa. Palibe vuto lidzagwera wolungama; koma amphulupulu adzadzazidwa ndi zoipa. Milomo yonama inyansa Yehova; koma ochita ntheradi amsekeretsa. Munthu wanzeru abisa zomwe adziwa; koma mtima wa opusa ulalikira utsiru. Dzanja la akhama lidzalamulira; koma waulesi adzakhala ngati kapolo. Nkhawa iweramitsa mtima wa munthu; koma mau abwino aukondweretsa. Wolungama atsogolera mnzake; koma njira ya oipa iwasokeretsa. Waulesi samaotcha nyama yake anaigwira; koma wolungama amalandira chuma chopambana cha anthu. M'khwalala la chilungamo muli moyo; m'njira ya mayendedwe ake mulibe imfa. Mwana wanzeru amamvera mwambo wa atate; koma wonyoza samvera chidzudzulo. Munthu adzadya zabwino ndi zipatso za m'kamwa mwake; koma moyo wa achiwembu udzadya chiwawa. Wogwira pakamwa pake asunga moyo wake; koma woyasamula milomo yake adzaonongeka. Moyo wa waulesi ukhumba osalandira kanthu; koma moyo wa akhama udzalemera. Wolungama ada mau onama; koma woipa anyansa, nadzichititsa manyazi. Chilungamo chitchinjiriza woongoka m'njira; koma udyo ugwetsa wochimwa. Alipo wodziyesa wolemera, koma alibe kanthu; alipo wodziyesa wosauka, koma ali ndi chuma chambiri. Chiombolo cha moyo wa munthu ndicho chuma chake; koma wosauka samva chidzudzulo. Kuunika kwa olungama kukondwa; koma nyali ya oipa idzazima. Kudzikuza kupikisanitsa; koma omwe anauzidwa uphungu ali ndi nzeru. Chuma cholandiridwa mokangaza chidzachepa; koma wokundika ndi dzanja adzaona zochuluka. Chiyembekezo chozengereza chidwalitsa mtima; koma pakufika chifunirocho ndicho mtengo wa moyo. Wonyoza mau adziononga yekha; koma woopa malangizo adzalandira mphotho. Malamulo a wanzeru ndiwo kasupe wa moyo, apatutsa kumisampha ya imfa. Nzeru yabwino ipatsa chisomo; koma njira ya achiwembu ili makolokoto. Yense wochenjera amachita mwanzeru; koma wopusa aonetsa utsiru. Mthenga wolakwa umagwa m'zoipa; koma mtumiki wokhulupirika alamitsa. Wokana mwambo adzasauka nanyozedwa; koma wolabadira chidzudzulo adzalemekezedwa. Chifuniro chikondweretsa moyo chitachitidwa; koma kusiya zoipa kunyansa opusa. Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzao wa opusa adzaphwetekedwa. Zoipa zilondola ochimwa; koma olungama adzalandira mphotho yabwino. Wabwino asiyira zidzukulu zake cholowa chabwino; koma wochimwa angosungira wolungama chuma chake. M'kulima kwa osauka muli zakudya zambiri; koma zinazo zimaonongeka posowa chiweruzo. Wolekerera mwanake osammenya amuda; koma womkonda amyambize kumlanga. Wolungama adya nakhutitsa moyo wake; koma mimba ya oipa idzasowa. Mkazi yense wanzeru amanga banja lake; koma wopusa alipasula ndi manja ake. Woyenda moongoka mtima aopa Yehova; koma wokhota m'njira yake amnyoza. M'kamwa mwa chitsiru muli nthyole ya kudzikuza; koma milomo ya anzeru idzawasunga. Popanda zoweta modyera muti see; koma mphamvu ya ng'ombe ichulukitsa phindu. Mboni yokhulupirika sidzanama; koma mboni yonyenga imalankhula zonama. Wonyoza afunafuna nzeru osaipeza; koma wozindikira saona vuto m'kuphunzira. Pita pamaso pa munthu wopusa, sudzazindikira milomo yakudziwa. Nzeru ya wochenjera ndiyo yakuti azindikire njira yake; koma utsiru wa opusa ndiwo chinyengo. Zitsiru zinyoza kupalamula; koma mwa oongoka mtima muli chiyanjano. Mtima udziwa kuwawa kwakekwake; mlendo sadudukira ndi chimwemwe chake. Nyumba ya oipa idzapasuka; koma hema wa oongoka mtima adzakula. Ilipo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka; koma matsiriziro ake ndi njira za imfa. Ngakhale m'kuseka mtima uwawa; ndipo matsiriziro a chiphwete ndi chisoni. Wobwerera m'mbuyo m'mtima adzakhuta njira yake; koma munthu wabwino adzakhuta za mwa iye yekha. Wachibwana akhulupirira mau onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake. Wanzeru amaopa nasiya zoipa; koma wopusa amanyada osatekeseka. Wokangaza kukwiya adzachita utsiru; ndipo munthu wa ziwembu adzadedwa. Achibwana amalandira cholowa cha utsiru; koma ochenjera amavala nzeru ngati korona. Oipa amagwadira abwino, ndi ochimwa pa makomo a olungama. Waumphawi adedwa ndi anzake omwe; koma akukonda wolemera achuluka. Wonyoza anzake achimwa; koma wochitira osauka chifundo adala. Kodi oganizira zoipa sasochera? Koma akuganizira zabwino adzalandira chifundo ndi ntheradi. M'ntchito zonse muli phindu; koma kulankhulalankhula kungopatsa umphawi. Korona wa anzeru ndi chuma chao; utsiru wa opusa ndiwo utsiru. Mboni yoona imalanditsa miyoyo; koma wolankhula zonama angonyenga. Wakuopa Yehova akhulupirira kolimba; ndipo ana ake adzakhala ndi pothawirapo. Kuopa Yehova ndiko kasupe wa moyo, kupatutsa kumisampha ya imfa. Mu unyinji wa anthu muli ulemu wa mfumu; koma popanda anthu kalonga aonongeka. Wosakwiya msanga apambana kumvetsa; koma wansontho akuza utsiru. Mtima wabwino ndi moyo wa thupi; koma nsanje ivunditsa mafupa. Wotsendereza aumphawi atonza Mlengi wake; koma wochitira wosauka chifundo amlemekeza. Wochimwa adzakankhidwa m'kuipa kwake; koma wolungama akhulupirirabe pomwalira. Nzeru ikhalabe m'mtima wa wozindikira, nidziwika pakati pa opusa. Chilungamo chikuza mtundu wa anthu; koma tchimo lichititsa fuko manyazi. Mfumu ikomera mtima kapolo wochita mwanzeru; koma idzakwiyira wochititsa manyazi. Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo; koma mau owawitsa aputa msunamo. Lilime la anzeru linena bwino zomwe adziwa; koma m'kamwa mwa opusa mutsanulira utsiru. Maso a Yehova ali ponseponse, nayang'anira oipa ndi abwino. Kuchiza lilime ndiko mtengo wa moyo; koma likakhota liswa moyo. Chitsiru chipeputsa mwambo wa atate wake; koma wosamalira chidzudzulo amachenjera. M'nyumba ya wolungama muli katundu wambiri; koma m'phindu la woipa muli vuto. Milomo ya anzeru iwanditsa nzeru, koma mtima wa opusa suli wolungama. Nsembe ya oipa inyansa Yehova; koma pemphero la oongoka mtima limkondweretsa. Njira ya oipa inyansa Yehova; koma akonda wolondola chilungamo. Wosiya njira adzalangidwa mowawa; wakuda chidzudzulo adzafa. Kumanda ndi kuchionongeko kuli pamaso pa Yehova; koposa kotani nanga mitima ya ana a anthu? Wonyoza sakonda kudzudzulidwa, samapita kwa anzeru. Mtima wokondwa usekeretsa nkhope; koma moyo umasweka ndi zowawa za m'mtima. Mtima wa wozindikira ufunitsa kudziwa; koma m'kamwa mwa opusa mudya utsiru. Masiku onse a wosauka ali oipa; koma wokondwera mtima ali ndi phwando losatha. Zapang'ono, ulikuopa Yehova, zipambana ndi katundu wambiri pokhala phokoso. Kudya masamba, pali chikondano, kuposa ng'ombe yonenepa pali udani. Munthu wozaza aputa makani; koma wosakwiya msanga atonthoza makangano. Mayendedwe a waulesi akunga linga laminga, koma njira ya oongoka mtima iundidwa ngati mseu. Mwana wanzeru akondweretsa atate wake; koma munthu wopusa apeputsa amake. Wosowa nzeru akondwera ndi utsiru; koma munthu wozindikira aongola mayendedwe ake. Zolingalira zizimidwa popanda upo; koma pochuluka aphungu zikhazikika. Munthu akondwera ndi mayankhidwe a m'kamwa mwake; ndi mau a pa nthawi yake kodi sali abwino? Anzeru ayesa njira yamoyo yokwerakwera, kuti apatuke kusiya kunsi kwa manda. Yehova adzapasula nyumba ya wonyada; koma adzalembera mkazi wamasiye malire ake. Ziwembu zoipa zinyansa Yehova; koma oyera mtima alankhula mau okondweretsa. Wopindula monyenga avuta nyumba yake; koma wakuda mitulo adzakhala ndi moyo. Mtima wa wolungama uganizira za mayankhidwe; koma m'kamwa mwa ochimwa mutsanulira zoipa. Yehova atalikira oipa; koma pemphero la olungama alimvera. Kuunika kwa maso kukondweretsa mtima; ndipo pomveka zabwino mafupa amatenga uwisi. Khutu lomvera chidzudzulo cha moyo lidzakhalabe mwa anzeru. Wokana mwambo apeputsa moyo wake; koma wosamalira chidzudzulo amatenga nzeru. Kuopa Yehova ndiko mwambo wanzeru; ndipo chifatso chitsogolera ulemu. Malongosoledwe a mtima nga munthu; koma mayankhidwe a lilime achokera kwa Yehova. Njira zonse za munthu ziyera pamaso pake; koma Yehova ayesa mizimu. Pereka zochita zako kwa Yehova, ndipo zolingalira zako zidzakhazikika. Zonse Yehova anazipanga zili ndi zifukwa zao; ngakhale amphulupulu kuti aone tsiku loipa. Yense wonyada mtima anyansa Yehova; zoonadi sadzapulumuka chilango. Mphulupulu iomboledwa ndi chifundo ndi ntheradi; apatuka pa zoipa poopa Yehova. Njira za munthu zikakonda Yehova ayanjanitsana naye ngakhale adani ake. Zapang'ono, pokhala chilungamo, ziposa phindu lalikulu lopanda chiweruzo. Mtima wa munthu ulingalira njira yake; koma Yehova ayendetsa mapazi ake. Mau a mlauli ali m'milomo ya mfumu; m'kamwa mwake simudzachita chetera poweruza. Mwini muyeso ndi mulingo wolungama ndiye Yehova; ndiyenso anapanga miyala yonse yoyesera ya m'thumba. Kuchita mphulupulu kunyansa mafumu; pakuti mpando wao wakhazikika ndi chilungamo. Milomo yolungama ikondweretsa mafumu; wonena zoongoka amkonda. Mkwiyo wa mfumu ndi mithenga ya imfa; wanzeru adzaukhulula. M'kuunika kwa nkhope ya mfumu muli moyo; kukoma mtima kwake kunga mtambo wa mvula ya masika. Kodi kulandira nzeru sikupambana ndi golide, kulandira luntha ndi kusankhika koposa siliva? Khwalala la oongoka mtima ndilo lakuti asiye zoipa; wosunga njira yake atchinjiriza moyo wake. Kunyada kutsogolera kuonongeka; mtima wodzikuza ndi kutsogolera kuphunthwa. Kufatsa mtima ndi osauka kuposa kugawana zofunkha ndi onyada. Wolabadira mau adzapeza bwino; ndipo wokhulupirira Yehova adala. Wanzeru mtima adzatchedwa wochenjera; ndipo kukoma kwa milomo kuonjezera kuphunzira. Nzeru ndi kasupe wa moyo kwa mwini wake; koma mwambo wa zitsiru ndi utsiru. Mtima wa wanzeru uchenjeza m'kamwa mwake, nuphunzitsanso milomo yake. Mau okoma ndiwo chisa cha uchi, otsekemera m'moyo ndi olamitsa mafupa. Ilipo njira yooneka kwa mwamuna ngati yoongoka, koma matsiriziro ake ndi njira za imfa. Wantchito adzigwirira yekha ntchito; pakuti m'kamwa mwake mumfulumiza. Munthu wopanda pake akonzeratu zoipa; ndipo m'milomo mwake muli moto wopsereza. Munthu wokhota amautsa makani; kazitape afetsa ubwenzi. Munthu wa chiwawa akopa mnzake, namuyendetsa m'njira yosakhala bwino. Wotsinzina ndiye aganizira zokhota; wosunama afikitsa zoipa. Imvi ndiyo korona wa ulemu, idzapezedwa m'njira ya chilungamo. Wosakwiya msanga aposa wamphamvu; wolamulira mtima wake naposa wolanda mudzi. Maere aponyedwa pamfunga; koma ndiye Yehova alongosola zonse. Nyenyeswa youma, pokhala mtendere, iposa nyumba yodzala nyama yansembe, pali makangano. Kapolo wochita mwanzeru adzalamulira mwana wochititsa manyazi, nadzagawana nao abale cholowa. Siliva ali ndi mbiya yosungunulira, golide ali ndi ng'anjo; koma Yehova ayesa mitima. Wochimwa amasamalira milomo yolakwa; wonama amvera lilime losakaza. Wochitira chiphwete aumphawi atonza Mlengi; wokondwera ndi tsoka sadzapulumuka chilango. Zidzukulu ndizo korona wa okalamba; ndipo ulemerero wa ana ndiwo atate ao. Mlomo wangwiro suyenera chitsiru; ngakhale mlomo wonama suyenera kalonga ndi pang'ono ponse. Wolandira chokometsera mlandu achiyesa ngale; paliponse popita iye achenjera. Wobisa cholakwa afunitsa chikondano; koma wobwerezabwereza mau afetsa ubwenzi. Chidzudzulo chilowa m'kati mwa wozindikira, kopambana ndi kukwapula wopusa kwambiri. Woipa amafuna kupanduka kokha; koma adzamtumizira mthenga wankhanza. Kukomana ndi chitsiru m'kupusa kwake kuopsa koposa chilombo chochichotsera anake. Wobwezera zabwino zoipa, zoipa sizidzamchokera kwao. Chiyambi cha ndeu chifanana ndi kutsegulira madzi; tsono kupikisana kusanayambe tasiya makani. Wokometsa mlandu wa wamphulupulu, ndi wotsutsa wolungama, onse awiriwa amnyansa Yehova. Kodi bwanji mtengo wogulira nzeru uli m'dzanja la chitsiru, popeza wopusa alibe mtima? Bwenzi limakonda nthawi zonse; ndipo mbale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka. Munthu wosowa nzeru apangana kulipirira wina, napereka chikole pamaso pa mnzake. Wokonda ndeu akonda kulakwa; ndipo wotalikitsa khomo lake afunafuna kuonongeka. Wokhota mtima sadzapeza bwino; ndipo mwini lilime lokhota adzagwa m'zoipa. Wobala chitsiru adzichititsa chisoni; ndipo atate wa wopusa sakondwa. Mtima wosekerera uchiritsa bwino; koma mzimu wosweka uphwetsa mafupa. Munthu woipa alandira chokometsera mlandu chotulutsa m'mfunga, kuti apatukitse mayendedwe a chiweruzo. Nzeru ili pamaso pa wozindikira; koma maso a wopusa ali m'malekezero a dziko. Mwana wopusa achititsa atate wake chisoni, namvetsa zowawa amake wombala. Kulipiritsa wolungama sikuli kwabwino, ngakhale kukwapula akulu chifukwa aongoka mtima. Wopanda chikamwakamwa apambana kudziwa; ndipo wofatsa mtima ali wanzeru. Ngakhale chitsiru chikatonthola achiyesa chanzeru; posunama ali wochenjera. Wopanduka afunafuna chifuniro chake, nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni. Wopusa sakondwera ndi kuzindikira; koma kungovumbulutsa za m'mtima mwake. Pakudza wamphulupulu padzanso kunyoza; manyazi natsagana ndi chitonzo. Mau a m'kamwa mwa munthu ndiwo madzi akuya; kasupe wa nzeru ndiye mtsinje wodzala. Kukometsa mlandu wa wamphulupulu mwatsankho sikuli kwabwino, ngakhale kuchitira chetera wolungama. Milomo ya wopusa ifikitsa makangano; ndipo m'kamwa mwake muputa kukwapulidwa. M'kamwa mwa wopusa mumuononga, milomo yake ikhala msampha wa moyo wake. Mau akazitape akunga zakudya zolongosoka, zotsikira m'kati mwa mimba. Wogwira ntchito mwaulesi ndiye mbale wake wa wosakaza. Dzina la Yehova ndilo nsanja yolimba; wolungama athamangiramo napulumuka. Chuma cha wolemera ndicho mudzi wake wolimba; alingalira kuti ndicho khoma lalitali. Mtima wa munthu unyada asanaonongeke; koma chifatso chitsogolera ulemu. Wobwezera mau asanamvetse apusa, nadzichititsa manyazi. Mtima wa munthu umlimbitsa alikudwala; koma ndani angatukule mtima wosweka? Mtima wa wozindikira umaphunzira; khutu la anzeru lifunitsa kudziwa. Mtulo wa munthu umtsegulira njira, numfikitsa pamaso pa akulu. Woyamba kudzinenera ayang'anika wolungama; koma mnzake afika namuululitsa zake zonse. Maere aletsa makangano, nulekanitsa amphamvu. Kupembedza mbale utamchimwira nkovuta, kulanda mudzi wolimba nkosavuta; makangano akunga mipiringidzo ya linga. Mimba ya munthu idzakhuta zipatso za m'kamwa mwake; iye nadzakhuta phindu la milomo yake. Lilime lili ndi mphamvu pa imfa ndi moyo; wolikonda adzadya zipatso zake. Wopeza mkazi apeza chinthu chabwino; Yehova amkomera mtima. Wosauka amadandaulira; koma wolemera ayankha mwaukali. Woyanjana ndi ambiri angodziononga; koma lilipo bwenzi lipambana ndi mbale kuumirira. Wosauka woyenda mwangwiro aposa wokhetsa milomo ndi wopusa. Kukhumba kosadziwa sikuli kwabwino; ndipo wofulumira ndi mapazi ake amachimwa. Utsiru wa munthu ukhotetsa njira yake; mtima wake udandaula pa Yehova. Chuma chionjezetsa mabwenzi ambiri; koma mnzake wa waumphawi amleka. Mboni yonama sidzakhala yosalangidwa; wolankhula mabodza sadzapulumuka. Ambiri adzapembedza waufulu; ndipo yense ndi bwenzi la munthu wopatsa. Abale onse a wosauka amuda; nanga mabwenzi ake kodi satanimphirana naye? Awatsata ndi mau, koma kuli zii. Wolandira nzeru akonda moyo wake; wosunga luntha adzapeza zabwino. Mboni yonama sidzapulumuka chilango; wolankhula mabodza adzaonongeka. Wopusa sayenera kukhala ndi zinthu zolongosoka; nanga kapolo ayenera kulamulira akalonga kodi? Kulingalira kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo; ulemerero wake uli wakuti akhululukire cholakwa. Mkwiyo wa mfumu ukunga kubangula kwa mkango; koma kukoma mtima kwake kunga mame pamsipu. Mwana wopusa ndiye tsoka la atate wake; ndipo makangano a mkazi ndiwo kudonthadonthabe. Nyumba ndi chuma ndizo cholowa cha atate; koma mkazi wanzeru achokera kwa Yehova. Ulesi ugonetsa tulo tofa nato; ndipo moyo wamkhongono udzamva njala. Wosunga lamulo asunga moyo wake; wonyalanyaza mayendedwe ake adzafa. Wochitira waumphawi chifundo abwereka Yehova; adzambwezera chokoma chakecho. Menya mwanako, chiyembekezero chilipo, osafunitsa kumuononga. Munthu waukali alipire mwini; pakuti ukampulumutsa udzateronso. Tamvera uphungu, nulandire mwambo, kuti ukhale wanzeru pa chimaliziro chako. Muli zolingalira zambiri m'mtima mwa munthu; koma uphungu wa Yehova ndiwo udzaimika. Chotikondetsa munthu ndicho kukoma mtima kwake; ndipo wosauka apambana munthu wonama. Kuopa Yehova kupatsa moyo; wokhala nako adzakhala wokhuta; zoipa sizidzamgwera. Waulesi alonga dzanja lake m'mbale, osalibwezanso kukamwa kwake. Menya wonyoza, ndipo achibwana adzachenjera; nudzudzule wozindikira adzazindikira nzeru. Wolanda za atate, ndi wopirikitsa amai, ndiye mwana wochititsa manyazi ndi wogwetsa nkhope. Ukangofuna, mwananga, kusochera kusiya mau akudziwitsa, leka kumva mwambo. Mboni yopanda pake inyoza chiweruzo; m'kamwa mwa amphulupulu mumeza zoipa. Akonzera onyoza chiweruzo, ndi mikwingwirima pamsana pa opusa. Vinyo achita chiphwete, chakumwa chaukali chisokosa; wosochera nazo alibe nzeru. Kuopsa kwa mfumu ndiko kubangula kwa mkango; womputa achimwira moyo wakewake. Kuli ulemu kwa mwamuna kupewa ndeu; koma zitsiru zonse zimangokangana. Waulesi salima chifukwa cha chisanu; adzapemphapempha m'masika osalandira kanthu. Uphungu wa m'mtima mwa munthu ndiwo madzi akuya; koma munthu wozindikira adzatungapo. Anthu ambiri abukitsa yense kukoma mtima kwake; koma ndani angapeze munthu wokhulupirika? Wolungama woyenda mwangwiro, anake adala pambuyo pake. Mfumu yokhala pa mpando woweruzira ipirikitsa zoipa zonse ndi maso ake. Ndani anganene, Ndasambitsa mtima wanga, ndayera opanda tchimo? Miyeso yosiyana, ndi malichero osiyana, zonse ziwirizi zinyansa Yehova. Ngakhale mwana adziwika ndi ntchito zake; ngati ntchito yake ili yoyera ngakhale yolungama. Khutu lakumva, ndi diso lopenya, Yehova anapanga onse awiriwo. Usakonde tulo ungasauke; phenyula maso, udzakhuta zakudya. Wogula ati, Chachabe chimenecho, koma atachoka adzitama. Alipo golide ndi ngale zambiri; koma milomo yodziwa ndiyo chokometsera cha mtengo wapatali. Tenga malaya a woperekera mlendo chikole; woperekera mkazi wachilendo chikole umgwire mwini. Zakudya za chinyengo zikondweretsa munthu; koma pambuyo pake m'kamwa mwake mudzadzala tinsangalabwi. Uphungu utsimikiza zolingalira, ponya nkhondo utapanga upo. Kazitape woyendayenda awanditsa zinsinsi; usadudukire woyasama milomo yake. Wotemberera atate wake ndi amake, nyali yake idzazima mu mdima woti bii. Cholowa chingalandiridwe msangamsanga poyamba pake; koma chitsiriziro chake sichidzadala. Usanene, Ndidzabwezera zoipa; yembekeza Yehova, adzakupulumutsa. Miyeso yosiyana inyansa Yehova, ndi mulingo wonyenga suli wabwino. Yehova alongosola mayendedwe a mwamuna; munthu tsono angazindikire bwanji njira yake? Kunena mwansontho, Ichi nchopatulika, kuli msampha kwa munthu, ndi kusinkhasinkha pambuyo pake atawinda. Mfumu yanzeru ipeta amphulupulu, niyendetsapo njinga ya galeta. Mzimu wa munthu ndiwo nyali ya Yehova; usanthula m'kati monse mwa mimba. Chifundo ndi ntheradi zisunga mfumu; chifundo chichirikiza mpando wake. Ulemerero wa anyamata ndiwo mphamvu yao; kukongola kwa nkhalamba ndi imvi. Mikwingwirima yopweteka ichotsa zoipa; ndi mikwapulo ilowa m'kati mwa mimba. Mtima wa mfumu uli m'dzanja la Yehova ngati mitsinje ya madzi; aulozetsa komwe afuna. Njira zonse za munthu zilungama pamaso pake; koma Yehova ayesa mitima. Kuchita chilungamo ndi chiweruzo kupambana ndi nsembe kumkonda Yehova. Maso akunyada, ndi mtima wodzikuza, ndi nyali ya oipa, zili tchimo. Zoganizira za wakhama zichulukitsadi katundu; koma yense wansontho angopeza umphawi. Kupata chuma ndi lilime lonama ndiko nkhungu yoyendayenda, ngakhale misampha ya imfa. Chiwawa cha amphulupulu chidzawakokolola; chifukwa akana kuchita chiweruzo. Wosenza tchimo njira yake ikhotakhota; koma ntchito ya woyera mtima ilungama. Kukhala pangodya ya tsindwi kufunika kuposa kukhala m'nyumba ndi mkazi wolongolola. Wamphulupulu mtima wake umkhumba zoipa; sakomera mtima mnzake. Polangidwa wonyoza, wachibwana alandira nzeru, naphunzira pakuyang'ana pa wanzeru. Wolungama aganizira za nyumba ya wamphulupulu, kuti amphulupulu amagwetsedwa, naona zoipa. Wotseka makutu ake polira waumphawi, nayenso adzalira koma osamvedwa. Mphatso ya m'tseri ipembedza mkwiyo, ndi mtulo wa pamfunga ukali wolimba. Kuchita chiweruzo kukondweretsa wolungama; koma kuwaononga akuchita mphulupulu. Munthu wosochera pa njira ya nzeru adzakhala m'msonkhano wa akufa. Wokonda zoseketsa adzasauka; wokonda vinyo ndi mafuta sadzalemera. Wochimwa ndiye chiombolo cha wolungama; ndipo wachiwembu adzalowa m'malo mwa oongoka mtima. Kukhala m'chipululu kufunika kuposa kukhala ndi mkazi wolongolola ndi wong'ung'udza. Mokhala wanzeru muli katundu wofunika ndi mafuta; koma wopusa angozimeza. Wolondola chilungamo ndi chifundo apeza moyo, ndi chilungamo, ndi ulemu. Wanzeru akwera pa mudzi wa olimba, nagwetsa mphamvu yake imene anaikhulupirira. Wosunga m'kamwa mwake ndi lilime lake asunga moyo wake kumavuto. Wonyada wodzikuza dzina lake ndiye wonyoza; achita mwaukali modzitama. Chifuniro cha waulesi chimupha; chifukwa manja ake akana kugwira ntchito. Ena asirira modukidwa tsiku lonse; koma wolungama amapatsa osamana. Nsembe ya oipa inyansa; makamaka pakudza nayo iwo mwachiwembu. Mboni yonama idzafa; koma mwamuna wakumvetsa adzanena mosakayika. Munthu woipa aumitsa nkhope yake; koma woongoka mtima akonza njira zake. Kulibe nzeru ngakhale luntha ngakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova. Kavalo amakonzedweratu chifukwa cha tsiku la nkhondo; koma wopulumutsa ndiye Yehova. Mbiri yabwino ifunika kopambana chuma chambiri; kukukomera mtima anzako kuposa siliva ndi golide. Wolemera ndi wosauka akumana, wolenga onsewo ndiye Yehova. Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa. Mphotho ya chifatso ndi kuopa Yehova ndiye chuma, ndi ulemu, ndi moyo. Minga ndi misampha ili m'njira ya wokhota; koma wosunga moyo wake adzatalikira imeneyo. Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo. Wolemera alamulira osauka; ndipo wokongola ndiye kapolo wa womkongoletsa. Wofesa zosalungama adzakolola tsoka; ndipo nthyole ya mkwiyo wake idzalephera. Mwini diso lamataya adzadala; pakuti apatsa osauka zakudya zake. Ukainga wonyoza, makangano adzatuluka; makani ndi manyazi adzalekeka. Wokonda kuyera mtima, mfumu idzakhala bwenzi lake chifukwa cha chisomo cha milomo yake. Maso a Yehova atchinjiriza wodziwa; koma agwetsa mau a munthu wa ziwembu. Waulesi ati, Pali mkango panjapo, ndidzaphedwa pamakwalalapo. M'kamwa mwa mkazi wachiwerewere muli dzenje lakuya; yemwe Yehova amkwiyira adzagwamo. Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana; koma nthyole yomlangira idzauingitsira kutali. Wotsendereza waumphawi kuti achulukitse chuma chake, ndi wopatsa wolemera kanthu, angosauka. Tchera makutu ako, numvere mau a anzeru, nulozetse mtima wako kukadziwa zanga. Pakuti mauwo akondweretsa ngati uwasunga m'kati mwako, ngati akhazikika pamodzi pa milomo yako. Ndakudziwitsa amenewo lero, ngakhale iwedi, kuti ukhulupirire Yehova. Kodi sindinakulembera zoposa za uphungu ndi nzeru; kuti ukadziwitse ntheradi yake ya mau oona, nukabwere ndi mau oona kwa iwo amene anakutumiza? Usalande za waumphawi chifukwa ali waumphawi, ngakhale kutsendereza wosauka kubwalo. Pakuti Yehova adzanenera mlandu wao; omwe akwatula zao Iye adzakwatula moyo wao. Usayanjane ndi munthu wokwiya msanga; ngakhale kupita ndi mwamuna waukali; kuti ungaphunzire mayendedwe ake, ndi kutengera moyo wako msampha. Usakhale wodulirana mpherere, ngakhale kumperekera chikole cha ngongole zake. Ngati ulibe chobwezera kodi achotserenji kama lako pansi pako? Usasunthe chidziwitso chakale cha m'malire, chimene makolo ako anachiimika. Kodi upenya munthu wofulumiza ntchito zake? Adzaima pamaso pa mafumu, osaima pamaso pa anthu achabe. Pamene ukhala ulinkudya ndi mkulu, zikumbukira ameneyo ali pamaso pako; nuike mpeni pakhosi pako, ngati uli wadyera. Usakhumbe zolongosoka zake; pokhala zakudya zonyenga. Usadzitopetse kuti ulemere; leka nzeru yakoyako. Kodi upenyeranji chimene kulibe? Pakuti chuma chimera mapiko, ngati mphungu youluka mumlengalenga. Usadye zakudya zake za wa maso ankhwenzule, ngakhale kukhumba zolongosoka zake. Pakuti monga asinkha m'kati mwake, ali wotere; ati kwa iwe, Idya numwe; koma mtima wake suli pa iwe. Pakuti nthongo imene unaidya udzaisanza, ndi kutaya mau ako okondweretsa. Usalankhule m'makutu a wopusa; pakuti adzapeputsa nzeru ya mau ako. Usasunthe chidziwitso chakale cha m'malire; ngakhale kulowa m'minda ya amasiye; pakuti Mombolo wao walimba; adzawanenera mlandu wao pa iwe. Lozetsa mtima wako kumwambo, ndi makutu ako ku mau anzeru. Usamane mwana chilango; pakuti ukammenya ndi nthyole safa ai. Udzammenya ndi nthyole, nudzapulumutsa moyo wake kunsi kwa manda. Mwananga, mtima wako ukakhala wanzeru, mtima wanga wa inedi udzakondwa. Imso zanga zidzasangalala, polankhula milomo yako zoongoka. Mtima wako usachitire nsanje akuchimwawo; koma opabe Yehova tsiku lonse. Pakutitu padzakhala mphotho; ndipo chiyembekezo chako sichidzalephereka. Tamvera tsopano, mwananga, utenge nzeru, ulunjikitse mtima wako m'njiramo. Usakhale mwa akumwaimwa vinyo, ndi ankhuli osusuka. Pakuti wakumwaimwa ndi wosusukayo adzasauka; ndipo kusinza kudzaveka munthu nsanza. Tamvera atate wako anakubala, usapeputse amai ako atakalamba. Gula ntheradi, osaigulitsa; nzeru, ndi mwambo, ndi luntha. Atate wa wolungama adzasekeradi; wobala mwana wanzeru adzakondwera naye. Atate wako ndi amai ako akondwere, amai ako akukubala asekere. Mwananga, undipatse mtima wako, maso ako akondwere ndi njira zanga. Pakuti mkazi wadama ndiye dzenje lakuya; ndipo mkazi wachiwerewere ndiye mbuna yopapatiza. Pakuti abisalira ngati wachifwamba, nachulukitsa anthu a chiwembu. Ndani ali ndi chisoni? Ndani asauka? Ndani ali ndi makangano? Ndani ang'ung'udza? Ndani alasidwa chabe? Ndani afiira maso? Ngamene achedwa pali vinyo, napita kukafunafuna vinyo wosanganizidwa. Usayang'ane pavinyo alikufiira, alikung'azimira m'chikho, namweka mosalala. Pa chitsiriziro chake aluma ngati njoka, najompha ngati mamba. Maso ako adzaona zachilendo, mtima wako udzalankhula zokhota. Udzafanana ndi wina wogona pakati pa nyanja, pena wogona pa nsonga ya mlongoti wa ngalawa. Udzati, Anandimenya, osaphwetekedwa ine; anandikwapula, osamva ine; ndidzauka nthawi yanji? Ndidzafunafunanso vinyoyo. Usachitire nsanje anthu oipa, ngakhale kufuna kukhala nao; pakuti mtima wao ulingalira za chionongeko; milomo yao ilankhula za mphulupulu. Nzeru imangitsa nyumba; luntha liikhazikitsa. Kudziwa kudzaza zipinda zake ndi chuma chonse chofunika cha mtengo wake. Mwamuna wanzeru ngwamphamvu; munthu wodziwa ankabe nalimba. Pakuti udzaponya nkhondo yako ndi upo, ndi kupulumuka pochuluka aphungu. Nzeru italikira chitsiru; satsegula pakamwa kubwalo. Wolingalira zakuchita zoipa anthu adzamtcha wachiwembu. Maganizo opusa ndiwo tchimo; wonyoza anyansa anthu. Ukalefuka tsiku la tsoka mphamvu yako ichepa. Omwe atengedwa kuti akafe, uwapulumutse; omwe ati aphedwe, usaleke kuwalanditsa. Ukanena, Taonani, sitinadziwa chimenechi; kodi woyesa mitima sachizindikira ichi? Ndi wosunga moyo wako kodi sachidziwa? Ndipo kodi sabwezera munthu yense monga mwa machitidwe ake? Mwananga, idya uchi pakuti ngwabwino, ndi chisa chake chitsekemera m'kamwa mwako. Potero udzadziwa kuti nzeru ili yotero m'moyo wako; ngati waipeza padzakhala mphotho, ndipo chiyembekezo chako sichidzalephereka. Usabisalire, woipa iwe, pomanga wolungama; usapasule popuma iyepo. Pakuti wolungama amagwa kasanu ndi kawiri, nanyamukanso; koma oipa akhumudwa pomfikira tsoka. Usakondwere pakugwa mdani wako; mtima wako usasekere pokhumudwa iye; kuti Yehova angaone kukondwa kwako, ndi kukuyesa koipa, ndi kuleka kumkwiyira. Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa; ngakhale kuchitira nsanje amphulupulu. Pakuti woipayo sadzalandira mphotho; nyali ya amphulupulu idzazima. Mwananga, opa Yehova ndi mfumu yomwe, osadudukira anthu osinthasintha. Pakuti tsoka lao lidzaoneka modzidzimuka; ndipo ndani adziwa chionongeko cha zaka zao? Izinso zili za anzeru, poweruza chetera silili labwino. Wonena kwa woipa, Wolungama iwe; magulu a anthu adzamtemberera, mitundu ya anthu idzamkwiyira. Omwe amdzudzula adzasekera, nadzadalitsika ndithu. Wobwezera mau oongoka apsompsona milomo. Longosola ntchito yako panjapo, nuikonzeretu kumunda; pambuyo pake ndi kumanga nyumba yako. Usachitire mnzako umboni womtsutsa opanda chifukwa; kodi udzanyenga ndi milomo yako? Usanene, Ndidzamchitira zomwezo anandichitira ine ndidzabwereza munthuyo monga mwa machitidwe ake. Ndinapita pa munda wa waulesi, polima mphesa munthu wosowa nzeru. Taonani, ponsepo panamera minga, ndi kuwirirapo khwisa; tchinga lake lamiyala ndi kupasuka. Pamenepo ndinayang'ana ndi kuganizira, ndinaona ndi kulandira mwambo. Tulo tapang'ono, kungoodzera pang'ono, kungomanga manja pang'ono m'kugona, ndipo umphawi wako udzafika ngati mbala; ndi kusauka kwako ngati munthu wachikopa. Iyinso ndiyo miyambo ya Solomoni imene anthu a Hezekiya mfumu ya Yuda anailemba. Kubisa kanthu ndi ulemerero wa Mulungu; koma ulemerero wa mafumu ndi kusanthula kanthu. Pamlengalenga patalika, ndi padziko pakuya, koma mitima ya mafumu singasanthulike. Chotsera siliva mphala yake, mmisiri wa ng'anjo atulutsamo mbale. Chotsera woipa pamaso pa mfumu, mpando wake udzakhazikika m'chilungamo. Usadzitame pamaso pa mfumu, ngakhale kuima m'malo mwa akulu. Pakuti kunena kwa iwe, Takwera kuno, kupambana ndi kuti utsitsidwe pamaso pa kalonga, amene maso ako anamuona. Usatuluke mwansontho kukalimbana, ungalephere pa kutha kwake, atakuchititsa mnzako manyazi. Nena mlandu wako ndi mnzako, osawulula zinsinsi za mwini; kuti wakumva angakutonze, mbiri yako yoipa ndi kusachoka. Mau oyenera a pa nthawi yake akunga zipatso zagolide m'nsengwa zasiliva. Monga mphete yagolide ndi chipini chagolide woyengeka, momwemo wanzeru wodzudzula pa khutu lomvera. Monga chisanu cha chipale chofewa pa nthawi ya masika, momwemo mthenga wokhulupirika kwa amene anamtuma; atsitsimutsa moyo wa ambuyake. Monga mitambo ndi mphepo popanda mvula, momwemo ndiye wodzikweza ndi zipatso zake monyenga. Chipiriro chipembedza mkulu; lilime lofatsa lithyola fupa. Wapeza uchi kodi? Idyapo wokwanira, kuti ungakukole, nusanze. Phazi lako lilowe m'nyumba ya mnzako kamodzikamodzi; kuti angatope nawe ndi kukuda. Wochitira mnzake umboni wonama ndiye chibonga, ndi lupanga, ndi muvi wakuthwa. Kukhulupirira munthu wa chiwembu tsiku latsoka kunga dzino lothyoka ndi phazi loguluka. Monga wovula malaya tsiku lamphepo, ngakhale kuthira vinyo wosasa m'soda, momwemo woimbira nyimbo munthu wachisoni. Mdani wako akamva njala umdyetse, akamva ludzu ummwetse madzi. Pakuti udzaunjika makala amoto pamtu pake; ndipo Yehova adzakupatsa mphotho. Mphepo ya kumpoto ifikitsa mvula; chomwecho lilime losinjirira likwiyitsa nkhope. Kukhala pangodya ya tsindwi kufunika kuposa kukhala m'nyumba ndi mkazi wolongolola. Monga madzi ozizira kwa munthu wotopa, momwemo mau abwino akuchokera kudziko lakutali. Monga kasupe wopondedwa, ndi chitsime choonongeka, momwemo wolungama ngati agonjera woipa. Kudya uchi wambiri sikuli kwabwino; chomwecho kufunafuna ulemu wakowako sikuli ulemu. Wosalamulira mtima wake akunga mudzi wopasuka wopanda linga. Monga chipale chofewa m'malimwe, ndi mvula m'masika, momwemo ulemu suyenera chitsiru. Monga mpheta ilikuzungulira, ndi namzeze alikuuluka, momwemo temberero la pachabe silifikira. Chikoti chiyenera kavalo, ndi cham'kamwa chiyenera bulu, ndi nthyole iyenera pamsana pa zitsiru. Usayankhe chitsiru monga mwa utsiru wake, kuti ungafanane nacho iwe wekha. Yankha chitsiru monga mwa utsiru wake, kuti asadziyese wanzeru. Wotumiza mau ndi dzanja la chitsiru adula mapazi ake, namwa zompweteka. Miyendo ya wopunduka ili yolobodoka, momwemo mwambi m'kamwa mwa zitsiru. Monga thumba la ngale m'mulu wa miyala, momwemo wochitira chitsiru ulemu. Monga munga wolasa dzanja la woledzera, momwemo mwambi m'kamwa mwa zitsiru. Monga woponya mivi ndi kulasa onse, momwemo wolembera chitsiru, ndi wolembera omwe alikupita panjira. Monga galu abweranso kumasanzi ake, momwemo chitsiru chichitanso zopusa zake. Kodi uona munthu wodziyesa wanzeru? Ngakhale chitsiru chidzachenjera koma ameneyo ai. Waulesi ati, Mkango uli panjira, wobangulawo uli m'makwalala. Monga chitseko chikankhikira pa zitsulo za pamphuthu, momwemo waulesi agubuduka pakama pake. Waulesi alonga dzanja lake m'mbale; kumtopetsa kulibweza kukamwa kwake. Waulesi adziyesa wanzeru koposa anthu asanu ndi awiri akuyankha mozindikira. Wakungopita ndi kuvutika ndi ndeu yosakhala yake akunga wogwira makutu a galu. Monga woyaluka woponya nsakali, mivi, ndi imfa, momwemo wonyenga mnzake ndi kuti, ndi kusewera kumeneku. Posowa nkhuni moto ungozima; ndi popanda kazitape makangano angoleka. Monga makala ozizira pa makala akunyeka, ndi nkhuni pamoto; momwemo munthu wamakangano autsa ndeu. Mau a kazitape ndi zakudya zolongosoka zitsikira m'kati mwa mimba. Milomo yofunitsitsa ndi mtima woipa ikunga mbale yadothi anaimata ndi mphala yasiliva. Wakuda mnzake amanyenga ndi milomo yake; koma akundika chinyengo m'kati mwake. Pamene akometsa mau ake usamkhulupirire; pakuti m'mtima mwake muli zonyansa zisanu ndi ziwiri. Angakhale abisa udani wake pochenjera, koma udyo wake udzavumbulutsidwa posonkhana anthu. Wokumba dzenje adzagwamo, wogubuduza mwala, udzabweranso pa iye mwini. Lilime lonama lida omwewo linawasautsa; ndipo m'kamwa mosyasyalika mungoononga. Usanyadire zamawa, popeza sudziwa tsiku lina lidzabala chiyani? Wina akutume, si m'kamwa mwako ai; mlendo, si milomo ya iwe wekha. Mwala ulemera, mchenga ndiwo katundu; koma mkwiyo wa chitsiru upambana kulemera kwake. Kupweteka mtima nkwa nkhanza, mkwiyo usefuka; koma ndani angalakike ndi nsanje? Chidzudzulo chomveka chiposa chikondi chobisika. Kulasa kwa bwenzi kuli kokhulupirika; koma mdani apsompsona kawirikawiri. Mtima wokhuta upondereza chisa cha uchi; koma wakumva njala ayesa zowawa zonse zotsekemera. Monga mbalame yosochera kuchisa chake, momwemo munthu wosochera kumalo ake. Mafuta ndi zonunkhira zikondweretsa mtima, ndi ubwino wa bwenzi uteronso pakupangira uphungu. Mnzako, ndi mnzake wa atate wako, usawasiye; usanke kunyumba ya mbale wako tsiku la tsoka lako; mnansi wapafupi aposa mbale wakutali. Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza. Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa. Tenga malaya a woperekera mlendo chikole; woperekera mkazi wachiwerewere chikole umgwire mwini. Yemwe adalitsa mnzake ndi mau akulu pouka mamawa, anthu adzachiyesa chimenecho temberero. Kudonthadontha tsiku lamvula, ndi mkazi wolongolola ali amodzimodzi. Wofuna kumletsayo afuna kuletsa mphepo; dzanja lake lamanja lingogwira mafuta. Chitsulo chinola chitsulo; chomwecho munthu anola nkhope ya mnzake. Wosunga mkuyu adzadya zipatso zake; wosamalira ambuyake adzalemekezedwa. Monga m'madzi nkhope zionana, momwemo mitima ya anthu idziwana. Kunsi kwa manda ndi kuchionongeko sikukhuta; ngakhale maso a munthu sakhutai. Siliva asungunuka m'mbiya, ndi golide m'ng'anjo, motero chomwe munthu achitama adziwika nacho. Ungakhale ukonola chitsiru m'mtondo ndi munsi, pamodzi ndi mphale, koma utsiru wake sudzamchoka. Udziwitsitse zoweta zako zili bwanji, samalira magulu ako; pakuti chuma sichili chosatha; kodi korona alipobe mpaka mibadwomibadwo. Amatuta udzu, msipu uoneka, atchera masamba a kumapiri. Anaankhosa akuveka, atonde aombolera munda; mkaka wa mbuzi udzakukwanira kudya; ndi a pa banja lako ndi adzakazi ako. Woipa athawa palibe momthamangitsa; koma olungama alimba mtima ngati mkango. Pochimwa dziko akalonga ake achuluka; koma anthu ozindikira ndi odziwa alikhazikikitsa nthawi yaikulu. Munthu waumphawi wotsendereza osauka akunga mvula yamadzi yokokolola dzinthu. Omwe asiya chilamulo atama oipa; koma omwe asunga chilamulo akangana nao. Oipa samvetsetsa chiweruzo; koma omwe afuna Yehova amvetsetsa zonse. Waumphawi woyenda mwangwiro apambana ndi yemwe akhotetsa njira zake, angakhale alemera. Wosunga chilamulo ndiye mwana wozindikira; koma mnzao wa adyera achititsa atate wake manyazi. Wochulukitsa chuma chake, pokongoletsa ndi phindu, angokundikira yemwe achitira osauka chisoni. Wopewetsa khutu lake kuti asamve chilamulo, ngakhale pemphero lake linyansa. Wosocheretsa oongoka mtima alowe m'njira yoipa, adzagwa mwini m'dzenje lake; koma angwiro adzalandira cholowa chabwino. Wolemera adziyesa wanzeru; koma wosauka wozindikira aululitsa zake. Posekera olungama pali ulemerero wambiri; koma pouka oipa anthu amabisala. Wobisa machimo ake sadzaona mwai; koma wakuwavomereza, nawasiya adzachitidwa chifundo. Wodala munthu wakuopa kosalekeza; koma woumitsa mtima wake adzagwa m'zoipa. Monga mkango wobangula ndi chilombo choyendayenda, momwemo mfumu yoipa ya anthu osauka. Kalonga wosowa nzeru apambana kusautsa; koma yemwe ada chisiriro adzatanimphitsa moyo wake. Wopalamula mlandu wakupha munthu adzathawira kudzenje; asamuletse. Woyenda mwangwiro adzapulumuka; koma wokhota m'mayendedwe ake adzagwa posachedwa. Wolima munda wake zakudya zidzamkwanira; koma wotsata anthu opanda pake umphawi udzamkwanira. Munthu wokhulupirika ali ndi madalitso ambiri; koma wokangaza kulemera sadzapulumuka chilango. Chetera silili labwino, ngakhale kulakwa kuti ukadye kanthu. Mwini diso lankhwenzule akangaza kulemera, osadziwa kuti umphawi udzamfikira. Adzamkomera mtima wodzudzula m'tsogolo mwake, koposa wosyasyalika ndi lilime lake. Wobera atate wake, pena amake, nati, Palibe kulakwa; ndiye mnzake wa munthu wopasula. Wodukidwa mtima aputa makangano; koma wokhulupirira Yehova adzakula. Wokhulupirira mtima wakewake ali wopusa; koma woyenda mwanzeru adzapulumuka. Wogawira aumphawi sadzasowa; koma wophimba maso ake adzatembereredwa kwambiri. Pouka oipa anthu amabisala; koma pakufa amenewo olungama achuluka. Yemwe aumitsa khosi atadzudzulidwa kwambiri, adzasweka modzidzimuka, palibe chomchiritsa. Pochuluka olungama anthu akondwa; koma polamulira woipa anthu ausa moyo. Mwamuna wokonda nzeru akondweretsa atate wake; koma wotsagana ndi akazi adama amwaza chuma. Mfumu akhazikitsa dziko ndi chiweruzo; koma wosonkhetsa anthu mphatso alipululutsa. Wosyasyalika mnzake atcherera mapazi ake ukonde. M'kulakwa kwa woipa muli msampha; koma wolungama aimba, nakondwera. Wolungama asamalira mlandu wa osauka; koma woipa alibe nzeru yakuudziwa. Anthu onyoza atentha mudzi; koma anzeru alezetsa mkwiyo. Munthu wanzeru akatsutsana ndi munthu wopusa, ngakhale akwiya, ngakhale aseka, palibe mtendere. Anthu ankhanza ada wangwiro; koma oongoka mtima asamalira moyo wake. Chitsiru chivumbulutsa mkwiyo wake wonse; koma wanzeru auletsa nautontholetsa. Mkulu akamvera chinyengo, atumiki ake onse ali oipa. Waumphawi ndi wotsendereza akumana; Yehova apenyetsa maso a onse awiriwo. Mfumu yolamulira osauka mwantheradi, mpando wake udzakhazikika kufikira nthawi zonse. Nthyole ndi chidzudzulo zipatsa nzeru; koma mwana womlekerera achititsa amake manyazi. Pochuluka oipa zolakwa zichuluka; koma olungama adzaona kugwa kwao. Langiza mwana wako, ndipo adzakupumitsa; nadzasangalatsa moyo wako. Popanda chivumbulutso anthu amasauka; koma wosunga chilamulo adalitsika. Kapolo sangalangizidwe ndi mau, pakuti azindikira koma osavomera. Kodi uona munthu wansontho m'mau ake? Ngakhale chitsiru chidzachenjera, koma ameneyo ai. Yemwe alera kapolo wake mwa ufulu kuyambira ubwana wake, pambuyo pake adzadziyesa mwana wobala. Mwamuna wamkwiyo aputa makangano; waukali achuluka zolakwa. Kudzikuza kwa munthu kudzamchepetsa; koma wokhala ndi mtima wodzichepetsa adzalemekezedwa. Woyenda ndi mbala ada moyo wakewake; amva kulumbira, koma osawulula kanthu. Kuopa anthu kutchera msampha; koma wokhulupirira Yehova adzapulumuka. Ambiri afunafuna chiyanjano cha mkulu; koma chiweruzo cha munthu chichokera kwa Yehova. Munthu woipa anyansa olungama; ndipo woongoka m'njira anyansa wochimwa. Mau a Aguri mwana wa Yake; uthenga. Munthuyo anati, Ndadzitopetsa, Mulungu; ndadzitopetsa, Mulungu, ndathedwa; pakuti ndipambana anthu onse kupulukira, ndilibe luntha la munthu. Sindinaphunzira nzeru ngakhale kudziwa Woyerayo. Ndani anakwera kumwamba natsikanso? Ndani wakundika nafumbata mphepo? Ndani wamanga madzi m'malaya ake? Ndani wakhazikitsa matsiriziro onse a dziko? Dzina lake ndani? Dzina la mwanake ndani? Kapena udziwa. Mau onse a Mulungu ali oyengeka; ndiye chikopa cha iwo amene amkhulupirira. Usaonjezere kanthu pa mau ake, angakudzudzule, nungatsutsidwe kuti ulikunama. Zinthu ziwiri ndakupemphani, musandimane izo ndisanamwalire: Mundichotsere kutali zachabe ndi mabodza; musandipatse umphawi, ngakhale chuma, mundidyetse zakudya zondiyenera; ndingakhute ndi kukukanani, ndi kuti, Yehova ndani? Kapena ndingasauke ndi kuba, ndi kutchula dzina la Mulungu wanga pachabe. Usanamizire kapolo kwa mbuyake, kuti angakutemberere nawe ndi kutsutsidwa. Pali mbadwo wotemberera atate ao, osadalitsa amai ao. Pali mbadwo wodziyesa oyera, koma osasamba litsiro lao. Pali mbadwo wokwezatu maso ao, zikope zao ndi kutukula. Pali mbadwo mano ao akunga malupanga, zibwano zao zikunga mipeni; kuti adye osauka kuwachotsa kudziko, ndi aumphawi kuwachotsa mwa anthu. Msundu uli ndi ana akazi awiri ati, Patsa, patsa. Pali zinthu zitatu sizikhuta konse, ngakhale zinai sizinena, Kwatha: Manda, ndi chumba, dziko losakhuta madzi, ndi moto wosanena, Kwatha. Diso lochitira atate wake chiphwete, ndi kunyoza kumvera amake, makungubwi a kumtsinje adzalikolowola, ana a mphungu adzalidya. Zinthu zitatu zindithetsa nzeru, ngakhale zinai, sindizidziwa: Njira ya mphungu m'mlengalenga, njira ya njoka pamwala, njira ya ngalawa pakati pa nyanja, njira ya mwamuna ndi namwali. Chomwecho njira ya mkazi wachigololo; adya, napukuta pakamwa, nati, Sindinachita zoipa. Chifukwa cha zinthu zitatu dziko linthunthumira; ngakhale chifukwa cha zinai silingathe kupirira nazo; chifukwa cha kapolo pamene ali mfumu; ndi chitsiru chitakhuta zakudya; chifukwa cha mkazi wodedwa wokwatidwa; ndi mdzakazi amene adzalandira cholowa cha mbuyake. Zilipo zinai zili zazing'ono padziko; koma zipambana kukhala zanzeru: Nyerere ndi mtundu wosalimba, koma zitengeratu zakudya zao m'malimwe. Mbira ndi mtundu wopanda mphamvu, koma ziika nyumba zao m'matanthwe. Dzombe lilibe mfumu, koma lituluka lonse mabwalomabwalo. Buluzi ungamgwire m'manja, koma ali m'nyumba za mafumu. Pali zinthu zitatu ziyenda chinyachinya; ngakhale zinai ziyenda mwaufulu: Mkango umene uposa zilombo kulimba, supatukira chinthu chilichonse; tambala wolimba m'chuuno, ndi tonde, ndi mfumu yokhala ndi ankhondo ake. Ngati wapusa podzikweza, ngakhale kuganizira zoipa, tagwira pakamwa. Pakuti potakasa mkaka, mafuta ayengekapo; ndi popsinja mfuno, mwazi utulukamo, ndi polimbikira mkwiyo ndeu ionekamo. Mau a Lemuwele mfumu, uthenga umene amake anamphunzitsa. Chiyani mwananga, Chiyani mwana wa mimba yanga? Chiyani mwana wa zowinda zanga? Musapereke mphamvu yako kwa akazi, ngakhale kuyenda m'njira yoononga mafumu. Mafumu, Lemuwele, mafumu sayenera kumwa vinyo; akalonga sayenera kunena, Chakumwa chaukali chili kuti? Kuti angamwe, naiwale malamulo, naweruze mokhota anthu onse osautsidwa. Wofuna kufa umpatse chakumwa chaukali, ndi vinyo kwa owawa mtima; amwe, naiwale umphawi wake, osakumbukiranso vuto lake. Tsegula pakamwa pako, ukanenere wosalankhula, ndi mlandu wa amasiye onse. Tsegula pakamwa pako nuweruze molungama, nunenere osauka ndi aumphawi. Mkazi wangwiro ndani angampeze? Pakuti mtengo wake uposa ngale. Mtima wa mwamuna wake umkhulupirira, sadzasowa phindu. Mkaziyo amchitira zabwino, si zoipa, masiku onse a moyo wake. Afuna ubweya ndi thonje, nachita mofunitsa ndi manja ake. Akunga zombo za malonda; nakatenga zakudya zake kutali. Aukanso kusanake, napatsa banja lake zakudya, nagawira adzakazi ake ntchito. Asinkhasinkha za munda, naugula; naoka mipesa ndi zipatso za manja ake. Amanga m'chuuno mwake ndi mphamvu, nalimbitsa mikono yake. Azindikira kuti malonda ake ampindulira; nyali yake sizima usiku. Agwira njinga ya thonje ndi dzanja lake, nafumbata mtengo wake. Aolowera chikhato chake osauka; natambasulira aumphawi manja ake. Saopera banja lake chipale chofewa; pakuti banja lake lonse livala mlangali. Adzipangira zimbwi zamawangamawanga; navala bafuta ndi guta wofiirira. Mwamuna wake adziwika kubwalo, pokhala pakati pa akulu a dziko. Asoka malaya abafuta, nawagulitsa; napereka mipango kwa ogulitsa malonda. Avala mphamvu ndi ulemu; nangoseka nthawi ya m'tsogolo. Atsegula pakamwa pake ndi nzeru, ndipo chilangizo cha chifundo chili pa lilime lake. Ayang'anira mayendedwe a banja lake, sadya zakudya za ulesi. Anake adzanyamuka, nadzamutcha wodala; mwamuna wake namtama, nati, Ana akazi ambiri anachita mwangwiro, koma iwe uposa onsewo. Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi chabe; koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa. Mumpatse zipatso za manja ake; ndi ntchito zake zimtame kubwalo. Mau a Mlaliki, mwana wa Davide, mfumu ya m'Yerusalemu. Zachabechabe, ati Mlaliki; zachabechabe zonse ndi chabe. Kodi ntchito zake zonse munthu asauka nazo zimpindulira chiyani? Mbadwo wina upita, mbadwo wina nufika; koma dziko lingokhalabe masiku onse. Inde dzuwa lituluka, nililowa, nilifulumira komwe linatulukako. Kulowa kumwera ndi kuzungulira kumpoto zungulirezungulire imaomba mphepo; ibweranso monga mwa mazunguliridwe ake. Mitsinje yonse ithira m'nyanja, koma nyanja yosadzala; komwe imukira mitsinjeyo, komweko ibweranso. Zinthu zonse zilemetsa; munthu sakhoza kuzifotokoza; maso sakhuta m'kuona, ndi makutu sakhuta m'kumva. Chomwe chinaoneka chidzaonekanso; ndi chomwe chinachitidwa chidzachitidwanso; ndipo palibe kanthu katsopano pansi pano. Kodi pali kanthu unganene kuti, Taona katsopano aka? Kanalipo kale, kale lomwe tisanabadwe ife. Zoyamba zija sizikumbukiridwa; ngakhale zomwe zilinkudzazo, omwe adzakhalabe m'tsogolomo, sadzazikumbukirai. Ine Mlaliki ndinali mfumu ya Israele m'Yerusalemu. Ndipo ndinapereka mtima kufunafuna ndi nzeru, ndi kulondetsa zonse zimachitidwa pansi pa thambo; ntchito yovuta imeneyi Mulungu apatsa ana a anthu akasauke nayo. Ndaona ntchito zonse zipangidwa kunja kuno; ndipo zonsezo ndi chabe ndi kungosautsa mtima. Chokhotakhota sichingaongokenso; ndipo choperewera sichingawerengedwe. Ndinalankhula ndi mtima wanga, ndi kuti, Taona, ndakuza ndi kudzienjezera nzeru koposa onse anakhala m'Yerusalemu ndisanabadwe ine; inde mtima wanga wapenyera kwambiri nzeru ndi chidziwitso. Ndipo ndinapereka mtima kudziwa nzeru ndi kudziwa misala ndi utsiru; ndinazindikira kuti ichinso chingosautsa mtima. Pakuti m'nzeru yambiri muli chisoni chambiri; ndi yemwe aenjezera chidziwitso aenjezera zowawa. Ndinati mumtima mwanga, Tiyetu, ndikuyese ndi chimwemwe; tapenya tsono zabwino; ndipo taona, ichinso ndi chabe. Ndinati, Kuseka ndi masala; ndi chimwemwe kodi chichita chiyani? Ndinafuna mumtima mwanga kusangalatsa thupi langa ndi vinyo, mtima wanga ulikunditsogolera mwanzeru, ndi kugwira utsiru, kuti ndizindikire chabwinocho cha ana a anthu nchiyani chimene azichichita pansi pa thambo masiku onse a moyo wao. Ndinadzipangira zazikulu; ndinadzimangira nyumba; ndi kuoka mipesa; ndinakonza mphanje ndi minda yanga, ndi kuokamo mitengo ya zipatso za mitundumitundu; ndinadzipangira ndekha matamanda a madzi akuthirira madzi m'nkhalango momeramo mitengo; ndinadzitengera akapolo ndi adzakazi, ndinali ndi akapolo anabadwa kwanga; ndinalemeranso pokhala nazo zoweta zazikulu ndi zazing'ono kupambana onse anakhala m'Yerusalemu ndisanabadwe ine; ndinakundikanso siliva ndi golide ndi chuma cha mafumu ndi madera a dziko; ndinaitanitsa amuna ndi akazi akuimba ndi zokondweretsazo za ana a anthu, ndizo zoimbira za mitundumitundu. Ndinakula chikulire kupambana onse anali m'Yerusalemu ndisanabadwe ine; ndipo nzeru yanganso inakhala nanebe. Ndipo chilichonse maso anga anachifuna sindinawamana; sindinakaniza mtima wanga chimwemwe chilichonse pakuti mtima wanga unakondwera ndi ntchito zanga zonse; gawo langa la m'ntchito zanga zonse ndi limeneli. Pamenepo ndinayang'ana zonse manja anga anazipanga, ndi ntchito zonse ndinasauka pozigwira; ndipo taona, zonse zinali zachabechabe ndi kungosautsa mtima, ndipo kunalibe phindu kunja kuno. Ndipo ndinatembenuka kukayang'ana nzeru ndi misala ndi utsiru; pakuti yemwe angotsata mfumu angachite chiyani? Si chomwe chinachitidwa kale. Pamenepo ndinazindikira kuti nzeru ipambana utsiru kwambiri, monga kuunika kupambana mdima. Wanzeru maso ake ali m'mutu wake, koma chitsiru chiyenda mumdima; ndipo nanenso ndinazindikira kuti chomwe chiwagwera onsewo ndi chimodzi. Pamenepo ndinati mumtima mwanga, Chomwe chigwera chitsiru nanenso chindigwera; nanga bwanji ndinapambana kukhala wanzeru? Pamenepo ndinati mumtima mwanga kuti ichinso ndi chabe. Pakuti wanzeru saposa chitsiru kukumbukidwa nthawi zonse; pakuti zonse zooneka kale zidzaiwalika m'tsogolomo. Ndipo wanzeru amwalira bwanji ngati chitsirutu. Chifukwa chake ndinada moyo; pakuti ntchito azipanga kunja kuno zindisautsa; pakuti zonse ndi chabe ndi kungosautsa mtima. Ndipo ndinada ntchito zanga zonse ndinasauka nazo kunja kuno; pakuti ndidzamsiyira izo munthu wina amene adzanditsata. Ndipo ndani adziwa ngati adzakhala wanzeru pena chitsiru? Koma adzalamulira ntchito zanga zonse ndinasauka nazo, ndi kuzigwira mwanzeru kunja kuno. Ichinso ndi chabe. Ndipo ndinatembenuka ndi kukhululuka za ntchito zanga zonse ndasauka nazo kunja kuno. Pakuti pali munthu wina agwira ntchito mwanzeru ndi modziwa nadzipinduliramo; koma adzapereka gawo lake kwa munthu amene sanagwirepo ntchito. Ichinso ndi chabe ndi choipa chachikulu. Pakuti munthu ali ndi chiyani m'ntchito zake zonse, ndi m'kusauka kwa mtima wake amasauka nazozo kunja kuno? Pakuti masiku ake onse ndi zisoni, vuto lake ndi kumliritsa; ngakhale usiku mtima wake supuma. Ichinso ndi chabe. Kodi si chabwino kuti munthu adye namwe, naonetse moyo wake zabwino m'ntchito yake? Ichinso ndinachizindikira kuti chichokera kudzanja la Mulungu. Pakuti ndani angadye ndi kufulumirako, koposa ine. Pakuti yemwe Mulungu amuyesa wabwino ampatsa nzeru ndi chidziwitso ndi chimwemwe; koma wochimwa amlawitsa vuto la kusonkhanitsa ndi kukundika, kuti aperekere yemwe Mulungu amuyesa wabwino. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima. Kanthu kalikonse kali ndi nthawi yake ndi chofuna chilichonse cha pansi pa thambo chili ndi mphindi yake; mphindi yakubadwa ndi mphindi yakumwalira; mphindi yakubzala ndi mphindi yakuzula zobzalazo; mphindi yakupha ndi mphindi yakuchiza; mphindi yakupasula ndi mphindi yakumanga; mphindi yakugwa misozi ndi mphindi yakuseka; mphindi yakulira ndi mphindi yakuvina; mphindi yakutaya miyala ndi mphindi yakukundika miyala; mphindi yakufungatirana ndi mphindi yakuleka kufungatirana; mphindi yakufunafuna ndi mphindi yakumwazika; mphindi yakusunga ndi mphindi yakutaya; mphindi yakung'amba ndi mphindi yakusoka; mphindi yakutonthola ndi mphindi yakulankhula; mphindi yakukonda ndi mphindi yakudana; mphindi ya nkhondo ndi mphindi ya mtendere. Wogwira Ntchito aona phindu lanji m'chomsautsacho? Ndaona vuto limene Mulungu wapatsa ana a anthu kuti avutidwe nalo. Chinthu chilichonse anachikongoletsa pa mphindi yake; ndipo waika zamuyaya m'mitima yao ndipo palibe munthu angalondetse ntchito Mulungu wazipanga chiyambire mpaka chitsiriziro. Ndidziwa kuti iwo alibe ubwino, koma kukondwa ndi kuchita zabwino pokhala ndi moyo. Ndiponso kuti munthu yense adye namwe naone zabwino m'ntchito zake zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu. Ndidziwa kuti zonse Mulungu azichita zidzakhala kufikira nthawi zonse; sungaonjezepo kanthu, ngakhale kuchotsapo; Mulungu nazichita kuti anthu akaope pamaso pake. Chomwe chinaoneka, chilikuonekabe; ndi chomwe chidzaoneka chinachitidwa kale; Mulungu anasanthula zochitidwa kale. Ndiponso ndinaona kunja kuno malo akuweruza, komweko kuli zoipa; ndi malo a chilungamo, komweko kuli zoipa. Ndinati mumtima wanga, Mulungu adzaweruza wolungama ndi woipa; pakuti pamenepo pali mphindi ya zofuna zonse ndi ntchito zonse. Ndinati mumtima mwanga, kuti izi zichitika ndi ana a anthu, kuti Mulungu awayese ndi kuti akazindikire eni ake kuti ndiwo nyama za kuthengo. Pakuti chomwe chigwera ana a anthu chigweranso nyamazo; ngakhale chowagwera nchimodzimodzi; monga winayo angofa momwemo zinazo zifanso; inde onsewo ali ndi mpweya umodzi; ndipo munthu sapambana nyama pakuti zonse ndi chabe. Onse apita kumalo amodzi; onse achokera m'fumbi ndi onse abweranso kufumbi. Ndani adziwa mzimu wa ana a anthu wokwera kumwamba, ndi mzimu wa nyama wotsikira kunsi dziko? M'mwemo ndinazindikira kuti kulibe kanthu kabwino kopambana aka, kuti munthu akondwere ndi ntchito zake; pakuti gawo lake ndi limeneli; pakuti ndani adzamfikitsa kuona chomwe chidzachitidwa atafa iyeyo? Ndinabweranso tsono ndi kupenyera nsautso zonse zimachitidwa kunja kuno; ndipo taona, misozi ya otsenderezedwa, koma analibe wakuwatonthoza; ndipo akuwatsendereza anali ndi mphamvu koma iwowa analibe wakuwatonthoza. Ndipo ndinatama akufa atatha kufa kupambana amoyo omwe alipobe; inde yemwe sanabadwe konse aposa onse awiriwo popeza sanaone ntchito yoipa yochitidwa kunja kuno. Ndiponso ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zompindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima. Chitsiru chimanga manja ake, nichidya nyama yakeyake. Dzanja limodzi lodzala pali mtendere liposa manja awiri oti thoo pali vuto ndi kungosautsa mtima. Pamenepo ndinabwera ndi kupenyera zachabe kunja kuno. Pali mmodzi palibe wachiwiri; inde, alibe mwana ngakhale mbale; koma ntchito yake yonse ilibe chitsiriziro, ngakhale diso lake silikhuta chuma. Samati, Ndigwira ntchito ndi kumana moyo wanga zabwino chifukwa cha yani? Ichinso ndi chabe, inde, vuto lalikulu. Awiri aposa mmodzi; pakuti ali ndi mphotho yabwino m'ntchito zao. Pakuti akagwa, wina adzautsa mnzake; koma tsoka wakugwa wopanda womnyamutsa. Ndiponso awiri akagona limodzi afunditsana; koma mmodzi pa yekha kodi adzafunditsidwa bwanji? Ndipo wina akamlaka mmodziyo, awiri adzachilimika; ndipo chingwe cha m'khosi zitatu sichiduka msanga. Mnyamata wosauka ndi wanzeru apambana mfumu yokalamba ndi yopusa, imene sifunanso kulangidwa mwambo. Pakuti atuluka m'nyumba yandende kulowa ufumu; komanso yemwe abadwa m'dziko lake asauka. Ndinapenyera anthu onse amoyo akuyenda kunja kuno, kuti anali ndi mwana, wachiwiri, amene adzalowa m'malo mwake. Anthu onse sawerengeka, ngakhale onsewo anawalamulira; koma amene akudza m'mbuyo sadzakondwera naye. Ichinso ndi chabe nichisautsa mtima. Samalira phazi lako popita kunyumba ya Mulungu; pakuti kuyandikira kumvera kupambana kupereka nsembe za zitsiru; pakuti sizizindikira kuti zilikuchimwa. Usalankhule mwanthuku mtima wako, usafulumire kunena kanthu pamaso pa Mulungu; pakuti Mulungu ali kumwamba, iwe uli pansi; chifukwa chake mau ako akhale owerengeka. Pakuti loto lafika mwakuchuluka ntchito; ndipo mau a chitsiru mwakuchuluka maneno. Utawinda chiwindo kwa Mulungu, usachedwe kuchichita; pakuti sakondwera ndi zitsiru; chita chomwe unachiwindacho. Kusawinda kupambana kuwinda osachita. Usalole m'kamwa mwako muchimwitse thupi lako; usanene pamaso pa mthenga kuti, Ndinaphophonya; Mulungu akwiyire mau ako chifukwa ninji, naononge ntchito ya manja ako? Pakuti monga mu unyinji wa maloto muli zachabe motero mochuluka mau; koma dziopa Mulungu. Ukaona anthu alikutsendereza aumphawi, ndi kuchotsa chilungamo ndi chiweruzo mwachiwawa pa dera lina la dziko, usazizwepo; pakuti mkulu wopambana asamalira; ndipo alipo akulu ena oposa amenewo. Phindutu la dziko lipindulira onse; ngakhale mfumu munda umthandiza; Wokonda siliva sadzakhuta siliva; ngakhale wokonda chuma sadzakhuta phindu; ichinso ndi chabe. Pochuluka katundu, akudyapo achulukanso; nanga apindulira eni ake chiyani, koma kungopenyera ndi maso ao? Tulo ta munthu wogwira ntchito ntabwino, ngakhale adya pang'ono ngakhale zambiri; koma kukhuta kwa wolemera sikumgonetsa tulo. Pali choipa chovuta ndachiona kunja kuno, ndicho, chuma chilikupweteka eni ake pochikundika; koma chumacho chionongeka pomgwera tsoka; ndipo akabala mwana, m'dzanja lake mulibe kanthu. Monga anatuluka m'mimba ya amake, adzabweranso kupita wamaliseche, monga anadza osatenga kanthu pa ntchito zake, kakunyamula m'dzanja lake. Ichinso ndi choipa chowawa, chakuti adzangopita monse monga anadza; ndipo wodzisautsa chabe adzaona phindu lanji? Inde masiku ake onse amadya mumdima, nizimchulukira chisoni ndi nthenda ndi mkwiyo. Taonani, chomwe ine ndapenyera kukoma ndi kuyenera munthu ndiko kudya, ndi kumwa, ndi kukondwera ndi ntchito zake zonse asauka nazo kunja kuno, masiku onse a moyo wake umene Mulungu ampatsa; pokhala gawo lake limeneli. Inde yemwe Mulungu wamlemeretsa nampatsa chuma, namninkhanso mphamvu ya kudyapo, ndi kulandira gawo lake ndi kukondwera ndi ntchito zake; umenewu ndiwo mtulo wa Mulungu. Pakuti sadzakumbukira masiku a moyo wake kwambiri; chifukwa Mulungu amvomereza m'chimwemwe cha mtima wake. Pali choipa ndachiona kunja kuno chifalikira mwa anthu, munthu amene Mulungu wamlemeretsa nampatsa chuma ndi ulemu, mtima wake susowa kanthu kena ka zonse azifuna, koma Mulungu osampatsa mphamvu ya kudyapo, koma mlendo adyazo; ichi ndi chabe ndi nthenda yoipa. Chinkana munthu akabala ana makumi khumi, nakhala ndi moyo zaka zambiri, masiku a zaka zake ndi kuchuluka, koma mtima wake osakhuta zabwino, ndiponso alibe maliro; nditi, Nsenye iposa ameneyo; pakuti ikudza mwachabe, nichoka mumdima, mdima nukwirira dzina lake. Ngakhale dzuwa siliona ngakhale kulidziwa, imeneyi ipambana winayo kupuma; akakhala ndi moyo zaka zikwi ziwiri, koma osakondwera; kodi onse sapita kumalo amodzi? Ntchito zake zonse munthu angogwirira m'kamwa mwake, koma mtima wake sukhuta. Pakuti wanzeru ali ndi chiyani choposa chitsiru? Waumphawi wodziwa kuyenda pamaso pa amoyo ali ndi chiyani? Kupenya kwa maso kuposa kukhumba kwa mtima; ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima. Chomwe chinalipo chatchedwa dzina lake kale, chidziwika kuti ndiye munthu; sakhoza kulimbana ndi womposa mphamvu. Pokhala zinthu zambiri zingochulukitsa zachabe, kodi anthu aona phindu lanji? Pakuti ndani adziwa chomwe chili chabwino kwa munthu ali ndi moyo masiku onse a moyo wake wachabe umene autsiriza ngati mthunzi? Pakuti ndani adzauza munthu chimene chidzaoneka m'tsogolo mwake kunja kuno? Mbiri yabwino iposa zonunkhira zabwino; ndi tsiku lakumwalira liposa tsiku lakubadwa. Kunka kunyumba ya maliro kupambana kunka kunyumba ya madyerero; pakuti kujako ndi matsiriziro a anthu onse; ndipo omwe ali ndi moyo adzakumbukirapo. Chisoni chiposa kuseka; pakuti nkhope yakugwa ikonza mtima. Mtima wa anzeru uli m'nyumba ya maliro; koma mtima wa zitsiru uli m'nyumba ya kuseka. Kumva chidzudzulo cha anzeru kupambana kumva nyimbo ya zitsiru. Pakuti kuseka kwa chitsiru kunga minga ilikuthetheka pansi pa mphika; ichinso ndi chabe. Indetu nsautso uyalutsa wanzeru; ndi mtulo uipitsa mtima. Chitsiriziro cha kanthu chiposa chiyambi chake; wofatsa mtima apambana wodzikuza mtima. Usakangaze mumtima mwako kukwiya; pakuti mkwiyo ugona m'chifuwa cha zitsiru. Usanene, Kodi bwanji masiku akale anapambana ano? Pakuti sulikufunsa mwanzeru pamenepo. Nzeru ili yabwino pamodzi ndi cholowa; akuona dzuwa apindula nayo. Pakuti nzeru itchinjiriza monga ndalama zitchinjiriza; koma kudziwa kupambana, chifukwa nzeru isunga moyo wa eni ake. Tapenya ntchito ya Mulungu; pakuti ndani akhoza kulungamitsa chomwe iye anachikhotetsa? Tsiku la mwai kondwera, koma tsiku la tsoka lingirira; Mulungu waika ichi pambali pa chinzake, kuti anthu asapeze kanthu ka m'tsogolo mwao. Ndaona zonsezi masiku anga achabe; pali wolungama angofa m'chilungamo chake, ndipo pali woipa angokhalabe ndi moyo m'kuipa kwake. Usapambanitse kukhala wolungama; usakhale wanzeru koposa; bwanji ufuna kudziononga wekha? Usapambanitse kuipa, ngakhale kupusa; uferenji nthawi yako isanafike? Kuli kwabwino kugwira ichi; indetu, usachotsepo dzanja lako pakuti yemwe aopa Mulungu adzatuluka monsemo. Nzeru ilimbitsa wanzeru koposa akulu khumi akulamulira m'mudzi. Pakuti kulibe wolungama pansi pano amene achita zabwino osachimwa. Mau onsetu onenedwa usawalabadire; kuti usamve kapolo wako alikukutemberera; pakuti kawirikawiritu mtima wako udziwa kuti nawenso unatemberera ena. Ndayesa zonsezi ndi nzeru; ndinati, Ndidzakhala wanzeru; koma inanditalikira. Chakutali ndi chakuyadi, adzachipeza ndani? Ndinapotoka ndi mtima wanga womwe kudziwa ndi kusanthula ndi kufunafuna nzeru ndi malongosoledwe a zinthu, ndi kudziwa kuti udyo ndiwo utsiru, ndi kuti kupusa ndi misala; ndipo ndinapeza kanthu kowawa koposa imfa, ndiko mkazi amene ndiye msampha, mtima wake ukunga maukonde, manja ake ndiwo matangadza; yemwe Mulungu amuyesa wabwino adzapulumuka kwa iye; koma wochimwa adzagwidwa naye. Taonani, ichi ndachipeza, ati Mlalikiyo, m'kuphatikiza chinthu china ndi chinzake, ndikazindikire malongosoledwe ao; chomwe moyo wanga uchifuna chifunire, koma osachipezai ndi ichi, mwamuna mmodzi mwa chikwi ndinampezadi, koma mkazitu mwa onsewo sindinampeza. Taonani, ichi chokha ndachipeza kuti Mulungu analenga anthu oongoka mtima; koma iwowo afunafuna malongosoledwe a mitundumitundu. Ndani akunga wanzeru? Ndani adziwa tanthauzo la mau? Nzeru ya munthu iwalitsa nkhope yake, kuduwa kwa nkhope yake ndi kusanduka. Nditi, Sunga mau a mfumu, makamaka m'kulumbira Mulungu. Usakangaze kumchokera; usaumirire kanthu koipa; pakuti iyeyo amachita chomwe chimkonda. Pakuti mau a mfumu ali ndi mphamvu; ndipo ndani anganene kwa iye, Kodi uchita chiyani? Wosunga chilamulo sadzadziwa kanthu koipa; ndipo mtima wa munthu wanzeru udziwa nyengo ndi maweruzo; pakuti kanthu kalikonse kali ndi nthawi yake ndi chiweruzo chake; popeza zoipa za munthu zimchulukira; pakuti sadziwa chimene chidzakhala; pakuti ndani angamuuze nthawi yakuti chidzachitidwa? Kulibe munthu ali ndi mphamvu yolamulira mzimu ndi yakutsekereza mzimu; ngakhale mphamvu tsiku la imfa; munkhondo umo mulibe kumasuka; udyo sudzapulumutsa akuzolowerana nao. Zonsezi ndaziona ndi kuyang'anitsa mtima wanga ntchito zonse zichitidwa pansi pano; nthawi yakuti wina apweteka mnzake pomlamulira. Ndipo ndinaona oipa alikuikidwa m'manda ndi kupita; ndipo omwe anachita zolungama anachokera kumalo opatulika akumudzi nawaiwala; ichinso ndi chabe. Popeza sambwezera choipa chake posachedwa atamtsutsa munthu, ana a anthu atsimikizadi mitima yao kuchita zoipa. Angakhale wochimwa achita zoipa zambirimbiri, masiku ake ndi kuchuluka, koma ndidziwitsadi kuti omwe aopa Mulungu naopa pamaso pake adzapeza bwino; koma woipa sadzapeza bwino ngakhale kutanimphitsa masiku ake ngati mthunzi; chifukwa saopa pamaso pa Mulungu. Pali chinthu chachabe chimachitidwa pansi pano; chakuti alipo olungama amene aona zomwe ziyenera ntchito za oipa, ndipo alipo oipa amene aona zomwe ziyenera ntchito za olungama. Ndinati, Ichinso ndi chabe. Pompo ndinatama kusekaseka, pakuti munthu alibe kanthu kabwino pansi pano, koma kudya ndi kumwa, ndi kusekera; ndi kuti zimenezi zikhalebe naye m'vuto lake masiku onse a moyo wake umene Mulungu wampatsa pansi pano. Pompo ndinapereka mtima wanga kudziwa nzeru, ndi kupenya ntchito zichitidwa pansi pano; kuti anthu saona tulo konse ndi maso ao ngakhale usana ngakhale usiku; pamenepo ndinaona ntchito zonse za Mulungu kuti anthu sangalondole ntchito zichitidwa pansi pano; pakuti angakhale munthu ayesetsa kuzifunafuna koma sadzazipeza; indetu ngakhalenso wanzeru akati, ndidziwa, koma adzalephera kuzilondola. Pakuti zonsezi ndinazisunga mumtima ndikalondoletu zonsezi; kuti olungama ndi anzeru ndi ntchito zao ali m'manja a Mulungu; ngakhale kukonda ngakhale kudana anthu sadziwa; zonse zili m'tsogolo mwao. Zonse zigwera onse chimodzimodzi; kanthu kamodzi kangogwera wolungama ndi woipa; ngakhale wabwino ndi woyera ndi wodetsedwa; ngakhale wopereka nsembe ndi wosapereka konse; wabwino alingana ndi wochimwa; wolumbira ndi woopa lumbira. Ichi ndi choipa m'zonse zichitidwa pansi pano, chakuti kanthu kamodzi kagwera onse; indetu, mtimanso wa ana a anthu wadzala udyo, ndipo misala ili m'mtima wao akali ndi moyo, ndi pamenepo apita kwa akufa. Pakuti woyang'ana ndi amoyo onse ali nacho chiyembekezo; pakuti galu wamoyo aposa mkango wakufa. Pakuti amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bii, sadzalandira mphotho; pakuti angoiwalika. Chikondi chao ndi mdano wao ndi dumbo lao lomwe zatha tsopano; ndipo nthawi yamuyaya sagawa konse kanthu kalikonse kachitidwe pansi pano. Tiye, idya zakudya zako mokondwa, numwe vinyo wako mosekera mtima; pakuti Mulungu wavomerezeratu zochita zako. Zovala zako zikhale zoyera masiku onse; mutu wako usasowe mafuta. Khalani mokondwa ndi mkazi umkonda masiku onse a moyo wako wachabe, umene Mulungu wakupatsa pansi pano masiku ako onse achabe; pakuti ilo ndi gawo lako la m'moyo ndi m'ntchito zimene uvutika nazo pansi pano. Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako. Ndinabweranso ndi kuzindikira pansi pano kuti omwe atamanga msanga sapambana m'liwiro, ngakhale olimba sapambana m'nkhondo, ngakhale anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira bwino salemera, ngakhale odziwitsa sawakomera mtima; koma yense angoona zomgwera m'nthawi mwake. Pakuti munthu sadziwatu mphindi yake; monga nsomba zigwidwa m'ukonde woipa, ndi mbalame zikodwa mumsampha, momwemo ana a anthu amagwidwa ndi nthawi ya tsoka, ngati msampha umene uwagwera modzidzimuka. Ndaonanso nzeru pansi pano motero, ndipo inandionekera yaikulu; panali mudzi waung'ono muli anthu owerengeka; ndipo inadzako mfumu yaikulu, niizinga ndi nkhondo, nimangapo malinga akulu; koma anapezedwamo mwamuna wanzeru wosauka, yemweyo napulumutsa mudziwo ndi nzeru yake; koma panalibe anthu anakumbukira wosauka ameneyo. Pamenepo ndinati, Nzeru ipambana mphamvu; koma anyoza nzeru ya wosauka, osamvera mau ake. Mau a anzeru achete amveka koposa kufuula kwa wolamulira mwa zitsiru. Nzeru ipambana zida za nkhondo; koma wochimwa mmodzi aononga zabwino zambiri. Ntchentche zakufa zinunkhitsa moipa nizioletsa mafuta onunkhira a sing'anga; chomwecho kupusa kwapang'ono kuipitsa iye amene atchuka chifukwa cha nzeru ndi ulemu. Wanzeru, mtima wake uli kudzanja lake lamanja; koma chitsiru, mtima wake kulamanzere. Inde, poyendanso chitsiru panjira, nzeru yake imthera ndipo angoti kwa onse kuti, Ndine chitsiru. Ngati mkulu akukwiyira, usasiye malo ako; chifukwa chifatso chipembedza utachimwa kwambiri. Pali choipa ndachiona pansi pano, ngati kulakwa koyambira ndi mkulu; utsiru ukhazikika pamwamba penipeni, ndipo olemera angokhala mwamanyazi. Ndaona akapolo atakwera pa akavalo, ndi mafumu, alikuyenda pansi ngati akopolo. Wokumba mbuna adzagwamo; ndipo woboola mpanda njoka idzamluma. Wosendeza miyala adzaphwetekedwa nayo; wowaza nkhuni nadzitema. Chitsulo chikakhala chosathwa, ndipo ukaleka kunola, uzipambana kulimbikira; koma nzeru ipindulira pochenjeza. Njoka ikaluma isanalodzedwe, watsenga saona mphotho. Mau a m'kamwa mwa munthu wanzeru nga chisomo; koma milomo ya chitsiru idzachimeza. Chiyambi cha mau a m'kamwa mwake ndi utsiru; ndipo chimaliziro cha m'kamwa mwake ndi misala yoipa. Chitsiru chichulukitsanso mau; koma munthu sadziwa chimene chidzaoneka; ndipo ndani angamuuze chomwe chidzakhala m'tsogolo mwake? Ntchito ya zitsiru izitopetsa zonsezo, pakuti sichidziwa kunka kumudzi. Tsoka kwa dzikowe, pamene mfumu yako ndiye mwana, ndipo akalonga ako adyera mamawa! Mwai kwa dzikowe, pamene mfumu yako ndiye mwana wa aufulu, ndipo akalonga ako adya pa nthawi yoyenera akalimbe osati akaledzere ai. Tsindwi litewa ndi mphwai za eni ake; nyumba nidontha ndi ulesi wa manja. Amaphikira zakudya kuti asekere, vinyo nakondweretsa moyo; ndipo ndalama zivomera zonse. Usatemberere mfumu ngakhale poganizira; usatemberere wolemera m'chipinda chogona iwemo; pakuti mbalame ya mlengalenga idzanyamula mauwo, ndipo chouluka ndi mapiko chidzamveketsa zonenazo. Ponya zakudya zako pamadzi; udzazipeza popita masiku ambiri. Gawira asanu ndi awiri ngakhale asanu ndi atatu; pakuti sudziwa choipa chanji chidzaoneka pansi pano. Mitambo ikadzala mvula, itsanulira pansi; mtengo ukagwa kumwera pena kumpoto, pomwe unagwa mtengowo udzakhala pomwepo. Woyang'ana mphepo sadzafesa; ndi wopenya mitambo sadzakolola. Monga sudziwa njira ya mphepo, ngakhale makulidwe a mafupa m'mimba ya mkazi ali ndi pakati; momwemo sudziwa ntchito za Mulungu amene achita zonse. Mamawa fesa mbeu zako, madzulonso osapumitsa dzanja lako; pakuti sudziwa ziti zidzalola bwino ngakhale izizi, ngakhale izozo, kaya zonse ziwiri zidzakhala bwino. Indetu kuunika nkokoma, maso napeza bwino m'kuona dzuwa. Inde, munthu akakhala ndi moyo zaka zambiri, akondwere ndi zonsezo; koma akumbukire masiku amdima kuti adzachuluka. Zonse zilinkudza zili zachabe. Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe; mtima wako nukasangalale masiku a unyamata wako, nuyende m'njira za mtima wako, ndi monga maso ako aona; koma dziwitsa kuti Mulungu adzanena nawe mlandu wa zonsezi. Chifukwa chake chotsani zopweteka m'mtima mwako, nulekanitse zoipa ndi thupi lako; pakuti ubwana ndi unyamata ngwa chabe. Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako, asanadze masiku oipa, ngakhale zisanayandikire zakazo zakuti udzati, Sindikondwera nazo; ngakhale lisanade dzuwa, ndi kuunika, ndi mwezi, ndi nyenyezi, mitambo ndi kubweranso italeka mvula; tsikulo omwe asunga nyumba adzanthunthumira, amuna olimba nadzawerama, akupera nadzaleka poperewera, omwe ayang'ana pamazenera nadzadetsedwa; pa khomo lakunja padzatsekeka; potsika mau akupera, wina nanyamuka polira mbalame, ndipo akazi onse akuimba sadzamveka bwino; inde, adzaopa za pamwamba, panjira padzakhala zoopsa; katungurume adzaphuka, dzombe ndi kukoka miyendo, zilakolako ndi kutha; pakuti munthu apita kwao kwamuyaya, akulira maliro nayendayenda panja; chingwe chasiliva chisanaduke, ngakhale mbale yagolide isanasweke, ngakhale mtsuko usanaphwanyike kukasupe, ngakhale njinga yotungira madzi isanathyoke kuchitsime; fumbi ndi kubwera pansi pomwe linali kale, mzimu ndi kubwera kwa Mulungu amene anaupereka. Chabe zachabetu, ati Mlalikiyo; zonse ndi chabe. Ndiponso pokhala wanzeru Mlalikiyo anaphunzitsabe anthu nzeru; inde, anatchera makutu nafunafuna nalongosola miyambi yambiri. Mlalikiyo anasanthula akapeze mau okondweretsa, ndi zolemba zoongoka ngakhale mau oona. Mau a anzeru akunga zisonga, omwe akundika mau amene mbusa mmodzi awapatsa mau ao akunga misomali yokhomedwa zolimba. Pamodzi ndi izi, mwananga, tachenjezedwa; pakuti saleka kulemba mabuku ambiri; ndipo kuphunzira kwambiri kutopetsa thupi. Mau atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi. Pakuti Mulungu adzanena mlandu wa zochita zonse, ndi zobisika zonse, ngakhale zabwino ngakhale zoipa. Nyimbo yoposa, ndiyo ya Solomoni. Mnyamatayo andipsompsonetse ndi m'kamwa mwake; pakuti chikondi chako chiposa vinyo. Mafuta ako anunkhira bwino; dzina lako likunga mafuta onunkhira otsanulidwa; chifukwa chake anamwali akukonda. Undikoke; tikuthamangire; mfumu yandilowetsa m'zipinda zake: Tidzasangalala ndi kukondwera ndi iwe. Tidzatchula chikondi chako koposa vinyo: Akukonda molungama. Wakuda ine, koma wokongola, ana akazinu a ku Yerusalemu, ngati mahema a Kedara, ngati nsalu zotchinga za Solomoni. Musayang'ane pa ine, pakuti ndada, pakuti dzuwa landidetsa. Ana amuna a amai anandikwiyira, anandisungitsa minda yamipesa; koma munda wangawanga wamipesa sindinausunga. Ndiuze, iwe amene moyo wanga ukukonda, umaweta kuti gulu lako? Umaligonetsa kuti pakati pa usana? Pakuti ndikhalirenji ngati wosochera pambali pa magulu a anzako? Ngati sudziwa, mkaziwe woposa kukongola, dzituluka kukalondola bande la gululo, nukawete anaambuzi zako pambali pa mahema a abusa. Ndakulinganiza, wokondedwa wanga mnyamatawe, ngati akavalo a magaleta a Farao. Masaya ako akongola ndi nkhata zatsitsi, ndi khosi lako ndi zinganga za mkanda wonyezimira. Tidzakupangira nkhata zagolide ndi njumu zasiliva. Pokhala mfumu podyera pake, narido wanga ananunkhira. Wokondedwa wanga mnyamatayo ali kwa ine ngati thumba la mure, logona pakati pa mawere anga. Wokondedwa wanga ali kwa ine ngati chipukutu cha maluwa ofiira m'minda yamipesa ya ku Engedi. Taona, wakongolatu, bwenzi langa; namwaliwe taona, wakongola, maso ako akunga a nkhunda. Taona, wakongolatu, bwenzi langa, mnyamatawe, inde, wakongoletsa; pogona pathu mpa msipu. Mitanda ya nyumba zathu nja mikungudza, ndi mapaso athu nga mlombwa. Ndine duwa lofiira la ku Saroni, ngakhale kakombo wa kuzigwa. Ngati kakombo pakati pa minga momwemo wokondedwa wanga pakati pa ana akazi. Ngati maula pakati pa mitengo ya m'nkhalango, momwemo wokondedwa wanga pakati pa ana amuna. Ndinakondwa pakukhala pa mthunzi wake, zipatso zake zinatsekemera m'kamwa mwanga. Anandifikitsa kunyumba ya vinyo, mbendera yake yondizolimira inali chikondi. Mundilimbikitse ndi mphesa zouma, munditonthoze mtima ndi maula, pakuti ndadwala ndi chikondi. Dzanja lake lamanzere anditsamiritse kumutu, dzanja lake lamanja ndi kundifungatira. Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu, pali mphoyo, ndi mbawala za kuthengo, kuti musautse, ngakhale kugalamutsa chikondi, mpaka chikafuna mwini. Mau a wokondedwa wanga mnyamatayo! Taona, adza, alikulumpha pamapiri, alikujidimuka pazitunda. Wokondedwa wanga akunga mphoyo, pena mwana wa mbawala: Taona, aima patseri pakhoma lathu. Apenyera pazenera, nasuzumira pamade. Wokondedwa wanga analankhula, nati kwa ine, tauka, bwenzi langa, wokongola wanga, tiye. Pakuti, taona, chisanu chatha, mvula yapita yaleka; maluwa aoneka pansi; nthawi yoimba mbalame yafika, mau a njiwa namveka m'dziko lathu. Mkuyu utchetsa nkhuyu zake zosakhwima, mipesa niphuka, inunkhira bwino. Tauka, bwenzi langa, wokongola wangawe, tiyetu. Nkhunda yangawe, yokhala m'ming'alu ya thanthwe, mobisika motsetsereka, ndipenye nkhope yako, ndimve mau ako; pakuti mau ako ngokoma, nkhope yako ndi kukongola. Mutigwirire ankhandwe, ngakhale ang'ono, amene akuononga minda yamipesa; pakuti m'minda yathu yamipesa muphuka biriwiri. Wokondedwa wanga ndi wa ine, ine ndine wake: aweta zake pakati akakombo. Mpaka dzuwa litapepa, mithunzi ndi kutanimpha, bwera, bwenzi langawe, nukhale ngati mphoyo pena mwana wa mbawala pa mapiri a mipata. Usiku pamphasa panga ndinamfunafuna amene moyo wanga umkonda: Ndinamfunafuna, koma osampeza. Ndinati, Ndiuketu, ndiyendeyende m'mudzi, m'makwalala ndi m'mabwalo ake, ndimfunefune amene moyo wanga umkonda: Ndimfunafuna, koma osampeza. Alonda akuyendayenda m'mudzi anandipeza: Ndinati, Kodi munamuona amene moyo wanga umkonda? Nditawapitirira pang'ono, ndinampeza amene moyo wanga umkonda: Ndinamgwiriziza, osamfumbatula, mpaka nditamlowetsa m'nyumba ya amai, ngakhale m'chipinda cha wondibala. Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu, pali mphoyo, ndi mbawala ya kuthengo, kuti musautse, ngakhale kugalamutsa chikondi, mpaka chikafuna mwini. Ndaniyu akwera kutuluka m'chipululu ngati utsi wa tolo, wonunkhira ndi mure ndi lubani, ndi zonunkhiritsa zonse za wogulitsa? Taonani, ndi machila a Solomoni; pazingapo amuna amphamvu makumi asanu ndi limodzi, a mwa ngwazi za Israele. Onsewo agwira lupanga, nazolowera nkhondo: Yense ali ndi lupanga lake pantchafu pake, chifukwa cha upandu wa usiku. Solomoni mfumu anadzipangira machila okhalamo tsonga ndi matabwa a ku Lebanoni. Anapanga timilongoti take ndi siliva, cha pansi pake ndi golide, mpando wake ndi nsalu yofiirira, pakati pake panayalidwa za chikondi cha ana akazi a ku Yerusalemu. Tulukani, ana akazi inu a Ziyoni, mupenye Solomoni mfumu, ndi korona amake amamveka naye tsiku la ukwati wake, ngakhale tsiku lakukondwera mtima wake. Taona, wakongola, bwenzi langa, namwaliwe, taona, wakongola; maso ako akunga a nkhunda patseri pa chophimba chako. Tsitsi lako likunga gulu la mbuzi, zooneka pa phiri la Giliyadi. Mano ako akunga gulu la nkhosa zosengasenga, zokwera kuchokera kosamba; yonse ili ndi ana awiri, palibe imodzi yopoloza. Milomo yako ikunga mbota yofiira, m'kamwa mwako ndi kukoma: Palitsipa pako pakunga phande la khangaza paseli pa chophimba chako. Khosi lako likunga nsanja ya Davide anaimangira zida, apachikapo zikopa zikwi, ngakhale zikopa zonse za amuna amphamvu. Mawere ako awiri akunga ana awiri a nswala obadwa limodzi, akudya pakati pa akakombo. Mpaka dzuwa litapepa, mithunzi ndi kutanimpha, ndikamuka kuphiri la mure, ndi kuchitunda cha lubani. Wakongola monsemonse, wokondedwa wanga, namwaliwe, mulibe chilema mwa iwe. Idza nane kuchokera ku Lebanoni, mkwatibwi, kuchokera nane ku Lebanoni: Unguza pamwamba pa Amana, pa nsonga ya Seniri ndi Heremoni, pa ngaka za mikango, pa mapiri a anyalugwe. Walanda mtima wanga, mlongo wanga, mkwatibwi; walanda mtima wanga ndi diso lako limodzi, ndi chinganga chimodzi cha pakhosi pako. Ha, chikondi chako nchokongola, mlongo wanga, mkwatibwi! Kodi chikondi chako sichiposa vinyo? Kununkhira kwa mphoka yako ndi kuposa zonunkhiritsa za mitundumitundu! M'milomo yako, mkwatibwi, mukukha uchi, uchi ndi mkaka zili pansi pa lilime lako; kununkhira kwa zovala zako ndi kunga kununkhira kwa Lebanoni. Mlongo wanga, mkwatibwi ndiye munda wotsekedwa; ngati kasupe wotsekedwa, ndi chitsime chopikiza. Mphukira zako ndi munda wamakangaza, ndi zipatso zofunika, bonongwe ndi narido. Narido ndi chikasu, nzimbe ndi sinamoni, ndi mitengo yonse ya lubani; mure ndi khonje, ndi zonunkhiritsa zonse zomveka. Ndiwe kasupe wa m'minda, chitsime cha madzi amoyo, ndi mitsinje yoyenda yochokera ku Lebanoni. Galamuka, mphepo ya kumpoto iwe, nudze, mphepo iwe ya kumwera; nuombe pamunda panga, kuti zonunkhiritsa zake zitulukemo. Bwenzi langa mnyamatayo, alowe m'munda mwake, nadye zipatso zake zofunika. Ndalowa m'munda mwanga, mlongo wanga, mkwatibwi: Ndatchera mure wanga ndi zonunkhiritsa zanga; ndadya uchi wanga ndi chisa chake; ndamwa vinyo wanga ndi mkaka wanga. Idyani, atsamwalinu, imwani, mwetsani chikondi. Ndinagona tulo, koma mtima wanga unali maso: Ndi mau a bwenzi langa mnyamatayo agogoda, nati, nditsegulire, mlongo wanga, wokondedwa wanga, nkhunda yanga, wangwiro wanga: Pakuti pamtu panga padzala mame, patsitsi panga pali madontho a usiku. Ndinayankha kuti, Ndavula malaya anga, ndiwavalenso bwanji? Ndasuka mapazi anga; ndiwadetserenji? Bwenzi langa analonga dzanja lake pazenera, mtima wanga ndi kuguguda chifukwa cha iye. Ndinauka ndikatsegulire bwenzi langa; pamanja panga panakha mure. Ndi pa zala zanga madzi a mure, pa zogwirira za mpikizo. Ndinamtsegulira bwenzi langalo; koma ndinampeza, bwenzi langa atachoka. Moyo wanga unalefuka polankhula iye: Ndinamfunafuna, osampeza; ndinamuitana, koma sanandivomere. Alonda akuyenda m'mudzi anandipeza, nandikantha, nanditema; osunga makoma nandichotsera chophimba changa. Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu, mukapeza bwenzi langa, mudzamuuza chiyani? Kuti ndadwala ndi chikondi. Bwenzi lako aposa abwenzi ena bwanji, mkaziwe woposa kukongola? Bwenzi lako aposa abwenzi ena bwanji, kuti utilumbirira motero? Wokondedwa wanga ali woyera ndi wofiira, womveka mwa zikwi khumi. Mutu wake ukunga golide, woyengetsa, tsitsi lake lopotana, ndi lakuda ngati khungubwi. Ana a maso ake akunga nkhunda pambali pa mitsinje ya madzi; otsukidwa ndi mkaka, okhala pa mitsinje yodzala. Masaya ake akunga chitipula chobzalamo ndiwo, ngati mitumbira yoyangapo masamba onunkhira: Milomo yake ikunga akakombo, pakukhapo madzi a mure. Manja ake akunga zing'anda zagolide zoikamo zonyezimira zoti biriwiri. Thupi lake likunga chopanga cha minyanga cholemberapo masafiro. Miyendo yake ikunga zoimiritsa za mwala wonyezimira, zogwirika m'kamwa mwa golide: Maonekedwe ake akunga Lebanoni, okometsetsa ngati mikungudza. M'kamwa mwake muli mokoma; inde, ndiye wokondweretsa ndithu. Ameneyu ndi wokondedwa wanga, ameneyu ndi bwenzi langa, ana akazi inu a ku Yerusalemu. Bwenzi lako wapita kuti, mkaziwe woposa kukongola? Bwenzi lako wapatukira kuti, tikamfunefune pamodzi nawe? Bwenzi langa watsikira kumunda kwake, kuzitipula za mphoka, kukadya kumunda kwake, ndi kutchera akakombo. Ndine wake wa wokondedwa wanga, wokondedwa wanganso ndiye wa ine; aweta zake pakati pa akakombo. Wakongola, bwenzi langa, namwaliwe ngati Tiriza, wokoma ngati Yerusalemu, woopsa ngati nkhondo ndi mbendera. Undipambutsire maso ako, pakuti andiopetsa. Tsitsi lako likunga gulu la mbuzi, zigona pambali pa Giliyadi. Mano ako akunga gulu la nkhosa zazikazi, zikwera kuchokera kosamba; yonse ili ndi ana awiri, palibe imodzi yopoloza. Palitsipa pako pakunga phande la khangaza paseli pa chophimba chako. Alipo akazi akulu a mfumu makumi asanu ndi limodzi, kudza akazi aang'ono makumi asanu ndi atatu, ndi anamwali osawerengeka. Nkhunda yanga, wangwiro wangayu, ndiye mmodzi; ndiye wobadwa yekha wa amake; ndiye wosankhika wa wombala. Ana akazi anamuona, namutcha wodala; ngakhale akazi akulu a mfumu, ndi akazi aang'ono namtamanda. Nati, Ndaniyo atuluka ngati mbandakucha, wokongola ngati mwezi, woyera ngati dzuwa, woopsa ngati nkhondo ndi mbendera? Ndinatsikira kumunda wa mtedza, kukapenya msipu wa m'chigwa, kukapenya ngati pamipesa paphuka, ngati pamakangaza patuwa maluwa. Ndisanazindikire, moyo wanga unandiimika pakati pa magaleta a anthu anga aufulu. Anati, Bwera, bwera, Msulamiwe; bwera, bwera, tiyang'ane pa iwe. Muyang'aniranji pa Msulami, ngati pa masewero akuguba? Ha, mapazi ako akongola m'zikwakwata, mwana wamkaziwe wa mfumu! Pozinga m'chuuno mwako pakunga zonyezimira, ntchito ya manja a mmisiri waluso. Pamchombo pako pakunga chikho choulungika, chosasowamo vinyo wosanganika: Pamimba pako pakunga mulu wa tirigu wozingidwa ndi akakombo. Mawere ako akunga ana awiri a nswala anabadwa limodzi. Khosi lako likunga nsanja yaminyanga; maso ako akunga matawale a ku Hesiboni, a pa chipata cha Batirabimu; mphuno yako ikunga nsanja ya ku Lebanoni imene iloza ku Damasiko. Mutu wako ukunga Karimele, ndi tsitsi la pamtu pako likunga nsalu yofiirira; mfumu yamangidwa ndi nkhata zake ngati wam'nsinga. Ha, ndiwe wokongola ndi wofunika, bwenziwe, m'zokondweretsa! Msinkhu wakowu ukunga mgwalangwa, mawere ako akunga matsango amphesa. Ndinati, Ndikakwera pa mgwalangwapo, ndikagwira nthambi zake: Mawere ako ange ngati matsango amphesa, ndi kununkhira kwa mpweya wako ngati maula. M'kamwa mwako munge ngati vinyo woposa, womeza tseketseke bwenzi langa, wolankhulitsa milomo ya ogona tulo. Ndine wa wokondedwa wanga mnyamatayo, ndine amene andifunayo. Tiye, bwenzi langa, tinke kuminda; titsotse m'milaga. Tilawire kunka kuminda yamipesa; tiyang'ane ngati mpesa waphuka, kunje ndi kuonetsa zipatso, makangaza ndi kutuwa maluwa ake; pompo ndidzakupatsa chikondi changa. Mankhwala a chikondi anunkhira, ndi pamakomo pathu zipatso zabwino, za mitundumitundu, zakale ndi zatsopano, zimene ndakukundikira iwe, wokondedwa wanga. Mwenzi utakhala ngati mlongo wanga, woyamwa pa bere la amai! Ndikadakupeza panja, ndikadakupsompsona; osandinyoza munthu. Ndikadakutsogolera, kukulowetsa m'nyumba ya amai, kuti andilange mwambo; ndikadakumwetsa vinyo wokoleretsa, ndi madzi a makangaza anga. Dzanja lamanzere lake akadanditsamiritsa kumutu, lamanja lake ndi kundifungatira. Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu, muutsiranji, mugalamutsiranji chikondi, chisanafune mwini. Ndaniyu achokera kuchipululu, alikutsamira bwenzi lake? Pa tsinde la muula ndinakugalamutsa mnyamatawe: Pomwepo amai ako anali mkusauka nawe, pomwepo wakukubala anali m'pakati pa iwe. Undilembe pamtima pako, mokhoma chizindikiro, nundikhomenso chizindikiro pamkono pako; pakuti chikondi chilimba ngati imfa; njiru imangouma ngati manda: Kung'anima kwake ndi kung'anima kwa moto, ngati mphezi ya Yehova. Madzi ambiri sangazimitse chikondi, ngakhale mitsinje yodzala kuchikokolola: Mwamuna akapereka katundu yense wa m'nyumba yake ngati sintho la chikondi, akanyozedwa ndithu. Tili ndi mlongwathu wamng'ono, alibe mawere; timchitirenji mlongo wathu tsiku lokhoma unkhoswe wake? Ngati ndiye khoma, tidzamanga pa iye nsanja yasiliva: Ngati ndiye chitseko tidzamtsekereza ndi matabwa amikungudza. Ndine khoma, mawere anga akunga nsanja zake: Pamaso pa mnyamatayo ndinafanana ngati wopeza mtendere. Solomoni anali ndi munda wamipesa ku Baala-Hamoni; nabwereka alimi mundawo; yense ambwezere ndalama chikwi chifukwa cha zipatso zake. Koma munda wanga wamipesa, uli pamaso panga ndiwo wangatu; nacho chikwicho, Solomoni iwe, koma olima zipatso zake azilandira mazana awiri. Namwaliwe wokhala m'minda, anzako amvera mau ako: Nanenanso undimvetse. Dzifulumira, mnyamatawe wokondedwa wanga, dzifanane ngati mphoyo pena mwana wa mbawala pa mapiri a mphoka. Masomphenya a Yesaya mwana wa Amozi, amene iye anaona, onena za Yuda ndi Yerusalemu, masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda. Imvani, miyamba inu, tchera makutu, iwe dziko lapansi, chifukwa Yehova wanena, Ndakulitsa ndipo ndalera ana, ndipo iwo anandipandukira Ine. Ng'ombe idziwa mwini wake, ndi bulu adziwa pomtsekereza: koma Israele sadziwa, anthu anga sazindikira. Mtundu wochimwa inu, anthu olemedwa ndi mphulupulu, mbeu yakuchita zoipa, ana amene achita moononga, iwo amsiya Yehova, iwo amnyoza Woyera wa Israele, iwo adana naye nabwerera m'mbuyo. Nanga bwanji mukali chimenyedwere kuti inu mulikupandukirabe? Mutu wonse ulikudwala, ndi mtima wonse walefuka. Kuchokera pansi pa phazi kufikira kumutu m'menemo mulibe changwiro; koma mabala, ndi mikwingwirima, ndi zilonda; sizinapole, ngakhale kumangidwa, ngakhale kupakidwa mafuta. Dziko lanu lili bwinja; midzi yanu yatenthedwa ndi moto; dziko lanu alendo alimkudya pamaso panu; ndipo lili labwinja monga lagubuduzidwa ndi alendo. Ndipo mwana wamkazi wa Ziyoni wasiyidwa ngati chitando cha m'munda wamphesa, chilindo cha m'munda waminkhaka, ngati mudzi wozingidwa ndi nkhondo. Akadapanda Yehova wa makamu kutisiyira otsala ang'onong'ono ndithu, ife tikanakhala ngati Sodomu, ife tikadanga Gomora. Imvani mau a Yehova inu olamulira a Sodomu, tcherani makutu ku chilamulo cha Mulungu wathu, inu anthu a Gomora. Nditani nazo nsembe zanu zochulukazo? Ati Yehova; ndakhuta nazo nsembe zopsereza za nkhosa zamphongo ndi mafuta a nyama zonenepa; sindisekera ndi mwazi wa ng'ombe zamphongo, ngakhale wa anaankhosa, ngakhale wa atonde. Pakudzaonekera inu pamaso pa Ine, ndani wafuna chimenechi m'dzanja lanu, kupondaponda m'mabwalo mwanga? Musadze nazonso, nsembe zachabechabe; nsembe zofukiza zindinyansa; tsiku lokhala mwezi ndi Sabata, kumema masonkhano, sindingalole mphulupulu ndi masonkhano. Masiku anu okhala mwezi ndi nthawi ya zikondwerero zanu mtima wanga uzida; zindivuta Ine; ndalema ndi kupirira nazo. Ndipo pamene mutambasula manja anu, ndidzakubisirani inu maso anga; inde pochulukitsa mapemphero anu Ine sindidzamva; manja anu adzala mwazi. Sambani, dziyeretseni; chotsani machitidwe anu oipa pamaso panga; lekani kuchita zoipa; phunzirani kuchita zabwino; funani chiweruzo; thandizani osautsidwa, weruzirani ana amasiye, munenere akazi amasiye. Tiyeni, tsono, tiweruzane, ati Yehova; ngakhale zoipa zanu zili zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale zili zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbu. Ngati inu muli ofuna ndi omvera, mudzadya zabwino za dziko, koma ngati mukana ndi kupanduka, mudzathedwa ndi lupanga; chifukwa m'kamwa mwa Yehova mwatero. Mudzi wokhulupirika wasanduka wadama! Wodzala chiweruzowo! Chilungamo chinakhalamo koma tsopano ambanda. Siliva wako wasanduka mphala, vinyo wako wasanganizidwa ndi madzi. Akulu ako apanduka, ali anzao a mbala; onse akonda mitulo, natsata zokometsera milandu; iwo saweruzira amasiye; ngakhale mlandu wa mkazi wamasiye suwafika. Chifukwa chake Yehova ati, Yehova wa makamu wamphamvu wa Israele, Ha! Ndidzatonthoza mtima wanga pochotsa ondivuta, ndi kubwezera chilango adani anga; ndipo ndidzaikanso dzanja langa pa iwe, ndi kukusungunula kukusiyanitsa iwe ndi mphala yako, ndipo ndidzachotsa seta wako wonse: ndidzabweza oweruza ako monga poyamba, ndi aphungu ako monga pachiyambi; pambuyo pake udzatchedwa Mudzi wolungama, mudzi wokhulupirika. Ziyoni adzaomboledwa ndi chiweruzo, ndi otembenuka mtima ake ndi chilungamo. Koma kupasula kwa olakwa ndi kwa ochimwa kudzakhala kumodzi, ndi iwo amene asiya Yehova adzathedwa. Chifukwa adzakhala ndi manyazi, chifukwa cha mitengo yathundu munaikhumba, ndipo inu mudzagwa nkhope, chifukwa cha minda imene mwaisankha. Chifukwa mudzakhala ngati mtengo wathundu, umene tsamba lake linyala, ngatinso munda wopanda madzi. Ndimo wamphamvu adzakhala ngati chingwe chathonje, ndi ntchito yake ngati nthethe; ndipo zonse zidzayaka moto pamodzi, opanda wozimitsa. Mau amene Yesaya mwana wa Amozi anaona, onena za Yuda ndi Yerusalemu. Ndipo padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pa nsonga ya mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko. Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kunka kuphiri la Yehova, kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m'mayendedwe ake; chifukwa m'Ziyoni mudzatuluka chilamulo, ndi mau a Yehova kuchokera m'Yerusalemu. Iye adzaweruza pakati pa akunja, adzadzudzula mitundu yambiri ya anthu; ndipo iwo adzasula malupanga ao akhale zolimira, ndi nthungo zao zikhale makasu; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo. Inu a nyumba ya Yakobo, tiyeni, tiyende m'kuwala kwa Yehova. Chifukwa inu mwasiya anthu anu a nyumba ya Yakobo, chifukwa kuti iwo adzazidwa ndi miyambo ya kum'mawa, ndipo ali olaula ngati Afilisti, naomba m'manja ndi ana a achilendo. Dziko lao ladzala siliva ndi golide, ngakhale chuma chao nchosawerengeka; dziko lao lidzalanso akavalo, ngakhale magaleta ao ngosawerengeka. Dziko lao ladzalanso mafano; iwo apembedza ntchito ya manja aoao, imene zala zaozao zinaipanga. Munthu wachabe agwada pansi, ndi munthu wamkulu adzichepetsa, koma musawakhululukire. Lowa m'phanga, bisala m'fumbi, kuchokera pa kuopsa kwa Yehova, ndi pa ulemerero wachifumu wake. Maso a munthu akuyang'anira kumwamba adzatsitsidwa, ndi kudzikweza kwa anthu kudzaweramitsidwa pansi; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa tsiku limenelo. Chifukwa padzakhala tsiku la Yehova wa makamu pa zonse zonyada ndi zakudzikuza, ndi pa zonse zotukulidwa; ndipo zidzatsitsidwa; ndi pa mitengo yonse yamkungudza ya Lebanoni, yaitali ndi yotukulidwa, ndi pa mitengo yonse yathundu ya Basani; ndi pa mapiri onse atali, ndi pa zitunda zonse zotukulidwa; ndi pa nsanja zazitali zonse, ndi pa machemba onse; ndi pa ngalawa zonse za Tarisisi, ndi pa zithunzithunzi zonse zokondweretsa. Ndipo kudzikweza kwa munthu kudzaweramitsidwa pansi, kudzikuza kwa munthu kudzatsitsidwa; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa tsiku limenelo. Ndimo mafano adzapita psiti. Anthu adzalowa m'mapanga a m'matanthwe, ndi m'maenje apansi, kuthawa kuopsa kwa Yehova, ndi ulemerero wachifumu wake, podzuka Iye kugwedeza dziko ndi mphamvu. Tsiku limenelo munthu adzataya kumfuko ndi kumileme mafano ake asiliva ndi agolide amene anthu anampangira iye awapembedze; kuti akalowe m'mapanga a m'matanthwe, ndi m'mindala a m'miyala, kuthawa kuopsa kwa Yehova, ndi ulemerero wachifumu wake, podzuka Iye kugwedeza dziko ndi mphamvu. Siyani munthu, amene mpweya wake uli m'mphuno mwake; chifukwa m'mene awerengedwamo ndi muti? Ndipo onani, Ambuye, Yehova wa makamu, wachotsa ku Yerusalemu ndi ku Yuda mchirikizo wochirikiza chakudya chonse ndi madzi onse, zimene zinali mchirikizo; munthu wamphamvu, ndi munthu wankhondo; woweruza ndi mneneri, ndi waula, ndi nkhalamba; kapitao wa makumi asanu, ndi munthu wolemekezeka, ndi mphungu, ndi mmisiri waluso, ndi wodziwa matsenga. Ndipo ndidzapereka ana, kuti akhale akulu ao, mwachibwana adzawalamulira. Ndi anthu adzavutidwa, yense ndi wina, yense ndi mnansi wake; mwana adzadzinyaditsa yekha pa akulu, ndi onyozeka pa olemekezedwa. Pamene mwamuna adzamgwira mbale wake m'nyumba ya atate wake, nadzati, Iwe uli ndi chovala, khala wolamulira wathu, ndi kupasula kumeneku kukhale m'dzanja lako; tsiku limenelo adzakweza mau ake, kuti, Sindine wochiritsa, chifukwa kuti m'nyumba mwanga mulibe chakudya kapena chovala; inu simudzandiyesa ine wolamulira anthu. Chifukwa kuti Yerusalemu wapasulidwa, ndi Yuda wagwa; chifukwa kuti lilime lao ndi machitidwe ao akana Yehova, kuti autse mkwiyo wa m'maso a ulemerero wake. Maonekedwe a nkhope zao awachitira iwo mboni; ndipo amaonetsa uchimo wao monga Sodomu, saubisa. Tsoka kwa moyo wao! Chifukwa iwo anadzichitira zoipa iwo okha. Nenani za wolungama, kuti kudzamkomera iye; chifukwa oterowo adzadya zipatso za machitidwe ao. Tsoka kwa woipa! Kudzamuipira; chifukwa kuti mphotho ya manja ake idzapatsidwa kwa iye. Anthu anga awavuta ndi ana, awalamulira ndi akazi. Anthu anga inu, iwo amene akutsogolerani, ndiwo akuchimwitsani, naononga njira zanu zoyendamo. Yehova aimirira kuti atsutsane, naimiriranso kuti aweruze mitundu ya anthu. Yehova adzalowa m'bwalo la milandu ndi okalamba a anthu ake, ndi akulu ake: Ndinu amene mwadya munda wamphesa, zofunkha za waumphawi zili m'nyumba zanu; muti bwanji inu, amene mupsinja anthu anga, ndi kupera nkhope ya wosauka? Ati Ambuye Yehova wa makamu. Komanso Yehova ati, Chifukwa kuti ana akazi a Ziyoni angodzikuza atakweza makosi ao, ndi maso ao adama nayenda nanyang'ama poyenda pao naliza zigwinjiri za mapazi ao; chifukwa chake Ambuye adzachita nkanambo pa liwombo la ana akazi a Ziyoni, ndipo Yehova adzavundukula m'chuuno mwao. Tsiku limenelo Ambuye adzachotsa zigwinjiri zao zokoma, ndi zitunga, ndi mphande; mbera, ndi makoza, ndi nsalu za pankhope; ndi zisada, ndi maunyolo a kumwendo, ndi mipango, ndi nsupa zonunkhira, ndi mphinjiri; mphete, ndi zipini; malaya a paphwando, ndi zofunda, ndi zimbwi, ndi timatumba; akalirole, ndi nsalu zabafuta, ndi nduwira, ndi zophimba. Ndipo padzakhala m'malo mwa zonunkhiritsa mudzakhala zovunda; ndi m'malo mwa lamba chingwe; ndipo m'malo mwa tsitsi labwino dazi; m'malo mwa chovala chapachifuwa mpango wachiguduli; zipsera m'malo mwa ukoma. Amuna ako adzagwa ndi lupanga, ndi wamphamvu wako m'nkhondo. Ndipo zipata zake zidzalira maliro; ndipo iye adzakhala bwinja, nadzakhala pansi. Ndipo akazi asanu ndi awiri adzagwira mwamuna mmodzi tsiku limenelo, nati, Ife tidzadya chakudya chathuchathu ndi kuvala zovala zathuzathu; koma titchedwe dzina lako; chotsa chitonzo chathu. Tsiku limenelo mphukira ya Yehova idzakhala yokongola ndi ya ulemerero, chipatso cha nthaka chidzakhala chokometsetsa ndi chokongola, kwa iwo amene adzapulumuka a Israele. Ndipo padzakhala, kuti iye amene asiyidwa m'Ziyoni, ndi iye amene atsala m'Yerusalemu adzatchedwa woyera; ngakhale yense amene walembedwa mwa amoyo m'Yerusalemu; pamene Ambuye adzasambitsa litsiro la ana akazi a Ziyoni, nadzatsuka mwazi wa Yerusalemu, kuchokera pakatipo, ndi mzimu wa chiweruziro, ndi mzimu wakutentha. Ndipo Yehova adzalenga pokhala ponse pa phiri la Ziyoni, ndi pa masonkhano ake, mtambo ndi utsi usana, ndi kung'azimira kwa malawi a moto usiku; chifukwa kuti pa ulemerero wonse padzayalidwa chophimba. Ndipo padzakhala chihema cha mthunzi, nthawi ya usana yopewera kutentha, pothawira ndi pousa mvula ndi mphepo. Ndiimbire wokondedwa wanga nyimbo ya wokondedwa wanga ya munda wake wamphesa. Wokondedwa wanga anali ndi munda wamphesa m'chitunda cha zipatso zambiri; ndipo iye anakumba mcherenje kuzungulira kwete, natolatola miyala pamenepo naokapo mpesa wosankhika, namangapo pakati pake nsanja, nasema mopondera mphesa, nayembekeza kuti udzabala mphesa, koma unangobala mphesa zosadya. Ndipo tsopano, inu okhala m'Yerusalemu, ndi anthu a Yuda, weruzanitu mlandu wa ine ndi munda wanga wamphesa. Ndikanachitanso chiyani ndi munda wanga wamphesa, chimene sindinachite m'menemo; muja ndinayembekeza kuti udzabala mphesa, wabaliranji mphesa zosadya? Ndipo tsopano ndidzakuuzani chimene nditi ndichite ndi munda wanga wamphesa; ndidzachotsapo tchinga lake, ndipo zidzadyedwa; ndidzagumula linga lake ndipo zidzapondedwa pansi; ndipo ndidzaupasula; sudzadzomboleredwa kapena kulimidwa; koma padzamera lunguzi ndi minga; ndidzalamuliranso mitambo kuti isavumbwepo mvula. Chifukwa kuti munda wamphesa wa Yehova wa makamu ndiwo banja la Israele, ndi anthu a Yuda, mtengo wake womkondweretsa; Iye nayembekeza chiweruziro, koma onani kuphana; nayembekeza chilungamo, koma onani kufuula. Tsoka kwa iwo amene aphatikiza nyumba ndi nyumba, amene alumikiza munda ndi munda, kufikira padzapanda malo, ndipo inu mudzasiyidwa nokha pakati pa dziko! M'makutu anga, ati Yehova wa makamu, Zoonadi nyumba zambiri zidzakhala bwinja, ngakhale zazikulu ndi zokoma zopanda wokhalamo. Chifukwa kuti munda wamphesa wa madera khumi udzangobala bati imodzi ya vinyo, ndi mbeu za maefa khumi zidzangobala efa imodzi. Tsoka kwa iwo amene adzuka m'mamawa kuti atsate zakumwa zaukali; amene achezera usiku kufikira vinyo awaledzeretsa! Ndipo zeze ndi mngoli, ndi lingaka ndi chitoliro, ndi vinyo, zili m'maphwando ao; koma iwo sapenyetsa ntchito ya Yehova; ngakhale kuyang'ana pa machitidwe a manja ake. Chifukwa chake anthu anga amuka m'nsinga, chifukwa cha kusowa nzeru; ndi amuna ao olemekezeka ali ndi njala, ndi khamu lao lauma kukhosi. Ndipo manda akuza chilakolako chake, natsegula kukamwa kwake kosayeseka; ndi ulemerero wao, ndi unyinji wao, ndi phokoso lao, ndi iye amene akondwerera mwa iwo atsikira mommo. Munthu wonyozeka waweramitsidwa, ndi munthu wotchuka watsitsidwa, ndi maso a wodzikweza atsitsidwa; koma Yehova wa makamu wakwezedwa m'chiweruziro, ndipo Mulungu Woyera wayeretsedwa m'chilungamo. Pamenepo anaankhosa adzadyapo ngati m'busa mwao, ndi malo a bwinja a zonenepa zachilendo zidzadyapo. Tsoka kwa iwo amene akoka mphulupulu ndi zingwe zachabe, ndi tchimo ngati ndi chingwe cha galeta; amene ati, Mlekeni iye akangaze, mlekeni iye afulumize ntchito yake kuti ife tione; ndipo lekani uphungu wa Woyera wa Israele uyandikire, udze kuti tiudziwe! Tsoka kwa iwo amene ayesa zoipa zabwino, ndi zabwino zoipa; amene aika mdima m'malo mwa kuyera, ndi kuyera m'malo mwa mdima; amene aika zowawa m'malo mwa zotsekemera, ndi zotsekemera m'malo mwa zowawa! Tsoka kwa iwo amene adziyesera anzeru ndi ochenjera! Tsoka kwa iwo amene ali a mphamvu yakumwa vinyo, ndi anthu olimba akusanganiza zakumwa zaukali; amene alungamitsa woipa pa chokometsera mlandu, nachotsera wolungama chilungamo chake! Chifukwa chake monga ngati lilime la moto likutha chiputu, ndi monga udzu wouma ugwa pansi m'malawi, momwemo muzu wao udzakhala monga wovunda, maluwa ao adzauluka m'mwamba ngati fumbi; chifukwa kuti iwo akana chilamulo cha Yehova wa makamu, nanyoza mau a Woyera wa Israele. Chifukwa chake mkwiyo wa Yehova wayaka pa anthu ake, ndipo Iye watambasulira iwo dzanja lake, nawakantha, ndipo zitunda zinanthunthumira, ndi mitembo yao inali ngati zinyatsi pakati pa makwalala. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire. Ndipo Iye adzakwezera a mitundu yakutali mbendera, nadzawaimbira mluzu, achokere ku malekezero a dziko; ndipo taonani, iwo adzadza ndi liwiro msangamsanga; palibe amene adzalema, kapena adzaphunthwa mwa iwo, palibe amene adzaodzera kapena kugona tulo; ngakhale lamba la m'chuuno mwao silidzamasuka, kapena chomangira cha nsapato zao sichidzaduka; amene mivi yao ili yakuthwa, ndi mauta ao onse athifuka; ziboda za akavalo ao zidzayesedwa ngati mwala, ndi njinga zao ngati kamvulumvulu; kubangula kwao kudzafanana ndi mkango, iwo adzabangula ngati ana a mikango, inde iwo adzabangula, nadzagwira nyama, naichotsa bwino opanda wakupulumutsa. Ndipo iwo adzawabangulira tsiku limenelo ngati kukokoma kwa nyanja; ndipo wina ayang'ana padziko, taonani mdima ndi nsautso, kuyera kwadetsedwanso m'mitambo yake. Chaka chimene mfumu Uziya anafa, ndinaona Ambuye atakhala pa mpando wachifumu wautali, ndi wotukulidwa, ndi zovala zake zinadzala m'Kachisi. Pamwamba pa Iye panaima aserafi; yense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi; awiri anaphimba nao nkhope yake, awiri naphimba nao mapazi ake, awiri nauluka nao. Ndipo wina anafuula kwa mnzake, nati, Woyera, Woyera, Woyera, Yehova wa makamu; dziko lonse lapansi ladzala ulemerero wake. Ndipo maziko a ziundo anasunthika ndi mau amene anafuula, ndipo nyumba inadzazidwa ndi utsi. Ndipo ine ndinati, Tsoka kwa ine! Chifukwa ndathedwa; chifukwa ndili munthu wa milomo yonyansa, ndikhala pakati pa anthu a milomo yonyansa; chifukwa kuti maso anga aona Mfumu, Yehova wa makamu. Pompo anaulukira kwa ine mmodzi wa aserafi, ali nalo khala lamoto m'dzanja mwake, limene analichotsa ndi mbaniro pa guwa la nsembe; nakhudza nalo kukamwa kwanga nati, Taona ichi chakhudza milomo yako; ndipo mphulupulu zako zachotsedwa, zochimwa zako zaomboledwa. Ndipo ndinamva mau a Ambuye akuti, Ndidzatumiza yani, ndipo ndani adzatimukira ife? Ndipo ine ndinati, Ndine pano; munditumize ine. Ndipo Iye anati, Kauze anthu awa, Imvani inu ndithu, koma osazindikira; yang'anani inu ndithu, koma osadziwitsa. Nenepetsa mtima wa anthu awa, lemeretsa makutu ao, nutseke maso ao; angaone ndi maso ao, angamve ndi makutu ao, angazindikire ndi mtima wao, nakabwerenso, nachiritsidwe. Pompo ndinati ine, Ambuye mpaka liti? Ndipo anayankha, Mpaka midzi ikhala bwinja, yopanda wokhalamo, ndi nyumba zopanda munthu, ndi dziko likhala bwinja ndithu, ndipo Yehova wasunthira anthu kutali, ndi mabwinja adzachuluka pakati pa dziko. Ndipo likatsala limodzi la magawo khumi m'menemo, lidzadyedwanso; monga kachere, ndi monganso thundu, imene tsinde lake likhalabe ataigwetsa; chotero mbeu yopatulika ndiyo tsinde lake. Ndipo panali masiku a Ahazi, mwana wa Yotamu, mwana wa Uziya, mfumu ya Yuda, kuti Rezini, mfumu ya Aramu, ndi Peka, mwana wa Remaliya, mfumu ya Israele, anakwera kunka ku Yerusalemu, kumenyana nao; koma sanathe kuupambana. Ndipo anauza a nyumba ya Davide, kuti Aramu wapangana ndi Efuremu. Ndipo mtima wake unagwedezeka, ndi mtima wa anthu ake, monga mitengo ya m'nkhalango igwedezeka ndi mphepo. Ndipo Yehova anati kwa Yesaya, Tuluka tsopano kukachingamira Ahazi, iwe ndi Seari-Yasubu, mwana wamwamuna wako, pa mamaliziro a mcherenje wa thamanda la pamtunda, kukhwalala la pa mwaniko wa wotsuka nsalu; nukati kwa iye, Chenjera, khala ulipo; usaope, mtima wako usalefuke, chifukwa cha zidutswa ziwirizi za miuni yofuka, chifukwa cha mkwiyo waukali wa Rezini ndi Aramu, ndi wa mwana wa Remaliya. Chifukwa Aramu ndi Efuremu, ndi mwana wa Remaliya anapangana kukuchitira zoipa, nati, Tiyeni, tikwere, timenyane ndi Yuda, timvute; tiyeni, tidzigumulire mpata, pamenepo tikhazike mfumu pakati pake, ngakhale mwana wamwamuna wa Tabeele; atero Ambuye Yehova, Upo wao sudzaimai, sudzachitidwa. Pakuti mutu wa Aramu ndi Damasiko, ndi mutu wa Damasiko ndi Rezini, zisadapite zaka makumi asanu ndi limodzi mphambu zisanu Efuremu adzathyokathyoka, sadzakhalanso mtundu wa anthu; ndipo mutu wa Efuremu ndi Samariya, ndi mutu wa Samariya ndi mwana wa Remaliya, mukapanda kukhulupirira ndithu simudzakhazikika. Ndipo Yehova ananenanso kwa Ahazi nati, Udzipemphere wekha chizindikiro cha kwa Yehova Mulungu wako; pempha cham'mwakuya, kapena cham'mwamba. Koma Ahazi anati, Sindipemphai ngakhale kumyesa Yehova. Ndipo iye anati, Mverani inu tsopano, inu a nyumba ya Davide; kodi ndi kanthu kakang'ono kwa inu kutopetsa anthu, kuti inu mutopetsa Mulungu wanga? Chifukwa chake Ambuye mwini yekha adzakupatsani inu chizindikiro; taonani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, nadzamutcha dzina lake Imanuele. Iye adzadya mafuta ndi uchi, pamene adziwa kukana choipa ndi kusankha chabwino. Popeza kuti asanadziwe mwanayo kukana choipa ndi kusankha chabwino, dziko limene mafumu ake awiri udana nao lidzasiyidwa. Yehova adzatengera pa iwe, ndi pa anthu ako, ndi pa nyumba ya atate wako, masiku, akuti sanadze oterewa kuyambira tsiku limene Efuremu analekana ndi Yuda; kunena mfumu ya Asiriya. Ndipo padzakhala tsiku limenelo kuti Yehova adzaimbira mluzu ntchentche ili m'mbali ya kumtunda kwa nyanja za Ejipito, ndi njuchi ili m'dziko la Asiriya. Ndipo zidzafika nizitera zonse m'zigwa zabwinja, ndi m'maenje a matanthwe, ndi paminga ponse, ndi pamabusa ponse. Tsiku limenelo Ambuye adzameta mutu, ndi ubweya wa m'mapazi, ndi lumo lobwereka lili tsidya lija la nyanja, kunena mfumu ya Asiriya; ndilo lidzamalizanso ndevu. Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti munthu adzaweta ng'ombe yaikazi yaing'ono, ndi nkhosa ziwiri; ndipo padzakhala, chifukwa cha kuchuluka kwa mkaka umene zidzapatsa, iye adzadya mafuta; pakuti mafuta ndi uchi adzadya yense wosiyidwa pakati pa dziko. Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti paliponse panali mipesa chikwi chimodzi ya mtengo wake wa sekeli chikwi chimodzi, padzakhala lunguzi ndi minga. Munthu adzafikako ndi mivi ndi uta; pakuti dziko lonse lidzakhala la lunguzi ndi minga. Ndipo zitunda zonse zinalimidwa ndi khasu, iwe sudzafikako chifukwa cha kuopa lunguzi ndi minga, koma pomwepo padzakhala potumizira ng'ombe ndi popondaponda nkhosa. Ndipo Yehova anati kwa ine, Tenga iwe polembapo papakulu, nulembe pamenepo ndi malembedwe odziwika, Kangazakufunkha Fulumirakusakaza. Ndipo ndidzadzitengera ine mboni zokhulupirika, Uriya wansembe, ndi Zekariya mwana wa Yeberekiya. Ndipo ndinanka kwa mneneri wamkazi; ndipo iye anatenga pakati nabala mwana wamwamuna. Ndipo Yehova anati kwa ine, Utche dzina lake, Kangazakufunkha Fulumirakusakaza. Chifukwa kuti mwana asakhale ndi nzeru yakufuula, Atate wanga, ndi Amai wanga, chuma cha Damasiko ndi chofunkha cha Samariya chidzalandidwa pamaso pa mfumu ya Asiriya. Ndipo Yehova ananena kwa ine kachiwirinso, nati, Popeza anthu awa akana madzi a Siloamu, amene ayenda pang'onopang'ono, nakondwerera mwa Rezini ndi mwa mwana wa Remaliya; chifukwa chake, taonani, Ambuye atengera pa iwo madzi a mtsinje wa Yufurate, olimba ndi ambiri, kunena mfumu ya Asiriya ndi ulemerero wake wonse; ndipo iye adzadzala mphaluka zake zonse, nadzasefukira pamtunda ponse. Ndipo iye adzapitapita kulowa m'Yuda; adzasefukira, napitirira; adzafikira m'khosi; ndi kutambasula kwa mapiko ake, kudzakwanira dziko lanu m'chitando mwake, inu Imanuele. Chitani phokoso, anthu inu, koma mudzathyokathyoka; tcherani khutu, inu nonse a maiko akutali; kwindani nokha, koma mudzathyokathyoka; kwindani nokha, koma mudzathyokathyoka. Panganani upo, koma udzakhala chabe; nenani mau, koma sadzachitika; pakuti Mulungu ali pamodzi ndi ife. Pakuti Yehova watero kwa ine ndi dzanja lolimba, nandilangiza ine kuti ndisayende m'njira ya anthu awa, nati, Musachinene, Chiwembu; chilichonse chimene anthu awa adzachinena, Chiwembu; musaope monga kuopa kwao kapena musachite mantha. Yehova wa makamu, Iye mudzamyeretsa; muope Iye, akuchititseni mantha Iye. Ndipo Iye adzakhala malo opatulika; koma mwala wophunthwitsa, ndi thanthwe lolakwitsa la nyumba zonse ziwiri za Israele, khwekhwe ndi msampha wa okhala m'Yerusalemu. Ndipo ambiri adzaphunthwapo, nagwa, nathyoka, nakodwa, natengedwa. Manga umboni, mata chizindikiro pachilamulo mwa aphunzi anga. Ndipo ndidzalindira Yehova, amene wabisira a nyumba ya Yakobo nkhope yake, ndipo ndidzamyembekeza Iye. Taonani, ine ndi ana amene Yehova wandipatsa ine, tili zizindikiro ndi zodabwitsa mwa Israele, kuchokera kwa Yehova wa makamu, amene akhala m'phiri la Ziyoni. Ndipo pamene iwo adzati kwa iwe, Funa kwa olaula, ndi obwebweta, amene alira pyepye, nang'ung'udza; kodi anthu sadzafuna kwa Mulungu wao? Chifukwa cha amoyo, kodi adzafuna kwa akufa? Kuchilamulo ndi kuumboni! Ngati iwo sanena malinga ndi mau awa, ndithu sadzaona mbandakucha. Ndipo iwo adzapitirira ovutidwa ndi anjala, ndipo padzakhala kuti pokhala ndi njala iwo adzadziputa okha, ndi kutemberera mfumu yao, ndi Mulungu wao; ndi kugadamira nkhope zao kumwamba; nadzayang'ana padziko, koma taonani, nkhawa ndi mdima, kuziya kwa nsautso; ndi mdima woti bii udzaingitsidwa. Koma kumene kunali nsautso sikudzakhala kuziya. Poyamba paja Mulungu ananyozetsa dziko la Zebuloni, ndi dziko la Nafutali, koma potsiriza pake Iye analichitira ulemu, pa khwalala la kunyanja, patsidya pa Yordani, Galileya wa amitundu. Anthu amene anayenda mumdima, aona kuwala kwakukulu; iwo amene anakhala m'dziko la mthunzi wa imfa, kuwala kwatulukira kwa iwo. Inu mwachulukitsa mtundu, inu mwaenjezera kukondwa kwao; iwo akondwa pamaso panu monga akondwera m'masika, monga anthu akondwa pogawana zofunkha. Pakuti goli la katundu wake, ndi mkunkhu wa paphewa pake, ndodo ya womsautsa, inu mwazithyola monga tsiku la Midiyani. Pakuti zida zonse za mwamuna wovala zida za nkhondo m'phokosomo, ndi zovala zovimvinika m'mwazi, zidzakhala zonyeka ngati nkhuni. Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere. Za kuenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, ndi kuuchirikiza ndi chiweruziro ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi. Ambuye anatumiza mau kwa Yakobo, ndipo anatsikira pa Israele. Ndipo anthu onse adzadziwa, ngakhale Efuremu ndi okhala m'Samariya, amene anena m'kunyada ndi m'kukula kwa mtima, Njerwa zagwa, koma ife tidzamanga ndi miyala yosema; mikuyu yagwetsedwa, koma tidzaisinthanitsa ndi mikungudza. Chifukwa chake Yehova adzamkwezera Rezini olimbana naye, nautsa adani ake; Aramu patsogolo ndi Afilisti pambuyo; ndipo iwo adzadya Israele ndi kukamwa koyasama. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire. Koma anthu sanatembenukire kwa Iye amene anawamenya, ngakhale kufuna Yehova wa makamu. Chifukwa chake Yehova adzadula mutu wa Israele ndi mchira wake; nthambi ya kanjedza ndi mlulu, tsiku limodzi. Nkhalamba ndi wolemekezeka ndiye mutu, ndi mneneri wophunzitsa zonama ndiye mchira. Pakuti iwo amene atsogolera anthuwa, ndiwo awasokeretsa; ndipo iwo amene atsogoleredwa nao aonongeka. Chifukwa chake Ambuye sadzakondwera ndi anyamata ao, ngakhale kuwachitira chifundo amasiye ao ana ndi akazi; popeza yense ali wodetsa ndi wochimwa, m'kamwa monse mulankhula zopusa. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire. Pakuti kuchimwa kwayaka ngati moto kumaliza lunguzi ndi minga, inde kuyaka m'nkhalango ya m'thengo, ndipo zifuka chapamwamba, m'mitambo yautsi yochindikira. M'kukwiya kwa Yehova wa makamu, dziko latenthedwa ndithu, anthunso ali ngati nkhuni; palibe munthu wochitira mbale wake chisoni. Ndipo wina adzakwatula ndi dzanja lamanja, nakhala ndi njala; ndipo adzadya ndi dzanja lamanzere, osakhutai; iwo adzadya munthu yense nyama ya mkono wake wa iye mwini. Manase adzadya Efuremu; ndi Efuremu adzadya Manase, ndipo iwo pamodzi adzadyana ndi Yuda. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire. Tsoka kwa iwo amene alamulira malamulo osalungama, ndi kwa alembi olemba mphulupulu; kuwapatulira osowa kuchiweruziro, ndi kuchotsera anthu anga aumphawi zoyenera zao, kuti alande za akazi amasiye, nafunkhire ana amasiye! Ndipo mudzachita chiyani tsiku lakudza woyang'anira, ndi chipasuko chochokera kutali? Mudzathawira kwa yani kufuna kuthangatidwa? Mudzasiya kuti ulemerero wanu? Adzangoweramira pansi pa andende, ndipo adzagwa pansi pa ophedwa. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire. Iwe Asiriya chibonga cha mkwiyo wanga, ndodo m'dzanja lake muli ukali wanga! Ine ndidzamtumiza kumenyana ndi mtundu wosalemekeza, ndi pa anthu a mkwiyo wanga ndidzamlangiza, kuti afunkhe, agwire zolanda, awapondereze pansi, monga dothi la pamakwalala. Koma iye safuna chotero, ndipo mtima wake suganizira chotero, koma mtima wake ulikufuna kusakaza, ndi kuduladula amitundu osawerengeka. Popeza ati, Akalonga anga kodi sali onse mafumu? Kodi Kalino sali wonga ngati Karikemisi? Kodi Hamati sali ngati Aripadi? Kodi Samariya sali ngati Damasiko? Popeza dzanja langa lapeza maufumu a mafano, mafano ao osema anapambana ndi iwo a ku Yerusalemu ndi ku Samariya; monga ndachitira Samariya ndi mafano ake, momwemo kodi sindidzachitira Yerusalemu ndi mafano ake? Chifukwa chake padzaoneka, kuti pamene Ambuye atatha ntchito yake yonse pa phiri la Ziyoni ndi pa Yerusalemu, ndidzalanga zipatso za mtima wolimba wa mfumu ya Asiriya, ndi ulemerero wa maso ake okwezedwa. Popeza anati, Mwa mphamvu ya dzanja langa ndachita ichi, ndi mwa nzeru yanga; pakuti ine ndili wochenjera; ndachotsa malekezero a anthu, ndalanda chuma chao, ndagwetsa monga munthu wolimba mtima iwo okhala pa mipando yachifumu; dzanja langa lapeza monga chisa, chuma cha mitundu ya anthu, ndipo monga munthu asonkhanitsa dziko lonse lapansi, ndipo panalibe chogwedeza phiko, kapena chotsegula pakamwa, kapena cholira pyepye. Kodi nkhwangwa idzadzikweza yokha, pa iye amene adula nayo? Kodi chochekera chidzadzikweza chokha pa iye amene achigwedeza, ngati chibonga ingamgwedeze iye amene ainyamula, ngati ndodo inganyamule kanthu popeza ili mtengo. Chifukwa chake Ambuye, Yehova wa makamu, adzatumiza kuonda mwa onenepa ake; ndipo pansi pa ulemerero wake padzayaka kutentha, konga ngati kutentha kwa moto. Ndipo kuwala kwa Israele kudzakhala moto, ndi Woyera wake adzakhala lawi; ndipo lidzatentha ndi kuthetsa minga yake ndi lunguzi wake tsiku limodzi. Ndipo adzanyeketsa ulemerero wa m'nkhalango yake, ndi wa m'munda wake wopatsa bwino, moyo ndi thupi; ndipo padzakhala monga ngati pokomoka wonyamula mbendera. Ndipo mitengo yotsala ya m'nkhalango yake idzakhala yowerengeka, kuti mwana ailembera. Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti otsala a Israele, ndi iwo amene anapulumuka a nyumba ya Yakobo, sadzatsamiranso iye amene anawamenya; koma adzatsamira Yehova Woyera wa Israele, ntheradi. Otsala adzabwera, otsala a Yakobo, kwa Mulungu wamphamvu. Popeza ngakhale anthu anu Israele akunga mchenga wa kunyanja, otsala ao okhaokha adzabwera; chionongeko chatsimikizidwa chilungamo chake chisefukira. Pakuti Ambuye Yehova wa makamu adzachita chionongeko chotsimikizidwa pakati pa dziko lonse lapansi. Chifukwa chake atero Ambuye Yehova wa makamu, Inu anthu anga okhala m'Ziyoni, musaope Asiriya; ngakhale amenya inu ndi chibonga, kapena kukusamulira iwe ndodo yake, monga amachitira Ejipito. Pakuti patsala kamphindi, ndipo ukali udzathedwa ndi mkwiyo wanga wakuwaononga. Ndipo Yehova wa makamu adzamuutsira chikoti, monga m'kuphedwa kwa Midiyani pa thanthwe la Orebu; ndipo chibonga chake chidzakhala pamwamba pa nyanja, ndipo adzaisamula monga anachitira Ejipito, Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti katundu wake adzachoka pa phewa lako, ndi goli lake pakhosi pako; ndipo goli lidzathedwa chifukwa cha kudzoza mafuta. Wafika ku Ayati, wapitirira kunka ku Migironi; pa Mikimasi asunga akatundu ake; wapita pampata; wagona pa Geba, Rama anthunthumira; Gibea wa Saulo wathawa. Fuula ndi mau ako iwe mwana wamkazi wa Galimu! Tamva, iwe Laisa! Iwe Anatoti wosauka! Madimena ali wothawathawa; okhala m'Gebimu asonkhana kuti athawe. Lero lomwe adzaima pa Nobu; agwedezera dzanja lake pa phiri la mwana wamkazi wa Ziyoni, phiri la Yerusalemu. Taonani, Ambuye Yehova wa makamu adzasadza nthambi moopsa; ndipo zazitali msinkhu zidzadulidwa, ndipo zazitali zidzagwetsedwa. Ndipo adzadula nkhalango za m'thengo ndi chitsulo, ndipo Lebanoni adzagwa ndi wamphamvu. Ndipo padzatuluka mphukira pa tsinde la Yese, ndi nthambi yotuluka m'mizu yake idzabala zipatso; Ndipo mzimu wa Yehova udzambalira iye mzimu wanzeru ndi wakuzindikira, mzimu wa uphungu ndi mphamvu, mzimu wakudziwa ndi wakuopa Yehova; ndipo adzakondwera nako kumuopa Yehova, ndipo sadzaweruza monga apenya maso, sadzadzudzula mwamphekesera: koma ndi chilungamo adzaweruza aumphawi, nadzadzudzulira ofatsa a m'dziko moongoka; ndipo adzamenya dziko lapansi ndi chibonga cha kukamwa kwake, nadzapha oipa ndi mpweya wa milomo yake. Ndipo chilungamo chidzakhala mpango wa m'chuuno mwake, ndi chikhulupiriko chidzakhala mpango wa pa zimpso zake. Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwanawankhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwanawambuzi; ndipo mwanawang'ombe ndi mwana wa mkango ndi choweta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng'ono adzazitsogolera. Ndipo ng'ombe yaikazi ndi chilombo zidzadya pamodzi; ndipo ana ao ang'ono adzagona pansi; ndipo mkango udzadya udzu ngati ng'ombe. Ndipo mwana wakuyamwa adzasewera pa una wa mamba, ndi mwana woleka kuyamwa adzaika dzanja lake m'funkha la mphiri. Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m'phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzaza ndi odziwa Yehova, monga mdazi adzaza nyanja. Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti muzu wa Yese umene uima ngati mbendera ya mitundu ya anthu, amitundu adzafunafuna uwu; ndipo popuma pake padzakhala ulemerero. Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti Ambuye adzabweza kachiwiri ndi dzanja lake anthu ake otsala ochokera ku Asiriya, ndi ku Ejipito, ndi ku Patirosi, ndi ku Kusi, ndi ku Elamu, ndi ku Sinara, ndi ku Hamati, ndi ku zisumbu za m'nyanja. Ndipo Iye adzaimika mbendera ya amitundu, ndipo adzasonkhanitsa oingitsidwa a Israele, namema obalalika a Yuda, kuchokera kumadera anai a dziko lapansi. Ndipo nsanje ya Efuremu idzachoka, ndi iwo amene avuta Yuda adzadulidwa; Efuremu sachitira nsanje Yuda, ndi Yuda sachitira nsanje Efuremu. Ndipo adzagudukira mapewa a Afilisti kumadzulo; pamodzi adzafunkha ana a kum'mawa; adzatambasula dzanja lao pa Edomu ndi pa Mowabu; ndipo ana a Amoni adzawamvera. Ndipo Yehova adzaononga ndithu bondo la nyanja ya Ejipito; ndipo ndi mphepo yake yopsereza adzagwedeza dzanja lake pa Mtsinje, ndipo adzaimenya ikhale mphaluka zisanu ndi ziwiri, nadzaolotsa anthu pansi pouma. Ndipo padzakhala khwalala la anthu ake otsala ochokera ku Asiriya; monga lija la Israele tsiku lokwera iwo kutuluka m'dziko la Ejipito. Tsiku lomwelo udzati, Ndikuyamikani inu Yehova; pakuti ngakhale munandikwiyira, mkwiyo wanu wachoka, ndipo mutonthoza mtima wanga. Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa. Chifukwa chake mudzakondwera pakutunga madzi m'zitsime za chipulumutso. Tsiku lomwelo mudzati, Muyamikire Yehova, bukitsani dzina lake, mulalikire machitidwe ake mwa mitundu ya anthu, munene kuti dzina lake lakwezedwa. Muimbire Yehova; pakuti wachita zaulemerero; chidziwike ichi m'dziko lonse. Tafuula, takuwa iwe, wokhala m'Ziyoni, chifukwa Woyera wa Israele wa m'kati mwako ali wamkulu. Katundu wa Babiloni, imene anaiona Yesaya mwana wa Amozi. Kwezani mbendera pa phiri loti see, kwezani mau kwa iwo, kodolani kuti alowe m'zipata za akulu. Ine ndalamulira opatulidwa anga, inde, ndaitana amphamvu anga, achite mkwiyo wanga, okondwerera ndi ukulu wanga. Mau a khamu m'mapiri, akunga a mtundu waukulu wa anthu, mau a phokoso la maufumu a mitundu yosonkhanidwa! Yehova wa makamu asonkhanitsa khamu kunkhondo. Achokera m'dziko lakutali, kumalekezero a thambo, ngakhale Yehova, ndi zida za mkwiyo wake, kuti aononge dziko lonse. Kuwani inu; pakuti tsiku la Yehova lili pafupi; lidzafika monga chionongeko chochokera kwa Wamphamvuyonse. Chifukwa chake manja onse adzafooka, ndi mitima yonse ya anthu idzasungunuka; ndipo adzaopa; zowawa ndi masauko zidzawagwira; ndipo adzamva zowawa, ngati mkazi wakubala; adzazizwa wina ndi wina; nkhope zao zidzanga malawi a moto. Taonani tsiku la Yehova lidza, lankhanza, ndi mkwiyo ndi kukalipira kwaukali; kupasula dziko, ndi kudzaonongamo akuchimwa psiti. Chifukwa nyenyezi za kumwamba ndi makamu ao sizidzawala; dzuwa lidzada m'kutuluka kwake, ndipo mwezi sudzaonetsa kuwala kwake. Ndipo ndidzalanga dziko lapansi, chifukwa cha kuipa kwao, ndi oipa chifukwa cha mphulupulu zao; ndipo ndidzaletsa kudzikuza kwa onyada, ndidzagwetsa kudzikweza kwa oopsa. Ndipo ndidzachepsa anthu koposa golide, ngakhale anthu koposa golide weniweni wa ku Ofiri. Chifukwa chake ndidzanthunthumiritsa miyamba, ndipo dziko lapansi lidzagwedezeka kuchokera m'malo ake, m'mkwiyo wa Yehova wa makamu, tsiku la mkwiyo wake waukali. Ndipo padzakhala kuti monga mbawala yothamangitsidwa, ndi monga nkhosa zosazisonkhanitsa anthu, adzatembenukira yense kwa anthu ake, nathawira yense kudziko lake. Onse opezedwa adzapyozedwa, ndi onse ogwidwa adzagwa ndi lupanga. Makanda ao adzatswanyidwe pamaso pao; m'nyumba mwao mudzafunkhidwa, ndi akazi ao adzakakamizidwa. Taonani, ndidzawautsira Amedi, amene sadzasamalira siliva, ngakhale golide sadzakondwera naye. Mauta ao adzatha anyamata; ndipo sadzachitira chisoni chipatso cha mimba; diso lao silidzaleka ana. Ndipo Babiloni, ulemerero wa maufumu, mudzi wokongolawo Ababiloni anaunyadira, adzakhala monga momwe Mulungu anapasula Sodomu ndi Gomora. Anthu sadzakhalamo konse, sadzakhalamo mbadwo ndi mbadwo; Mwarabu sadzamanga hema wake pamenepo; abusa sadzagonetsa makamu ao kumeneko. Koma zilombo za m'chipululu zidzagona pamenepo; nyumba zao zidzadzala ndi zakukuwa; ndipo nthiwatiwa zidzakhala pamenepo, ndipo atonde adzajidimuka pamenepo. Ndipo mimbulu idzalira m'maboma ao, ndi ankhandwe m'manyumba ao abwino; ndi nthawi yake iyandikira, ndi masiku ake sadzachuluka. Pakuti Ambuye adzamchitira chifundo Yakobo, ndipo adzasankhanso Israele, ndi kuwakhazikitsa m'dziko la kwao; ndipo achilendo adzadziphatika okha kwa iwo, nadzadzigumikiza kunyumba ya Yakobo. Ndipo mitundu ya anthu idzawatenga, ndi kuwafikitsa kumalo a kwao; ndipo a nyumba ya Israele adzakhala nao amitunduwo m'dziko la Yehova, ndi kuwayesa atumiki ndi adzakazi, ndipo amitunduwo adzatengedwa ndende, ndi amenewo anali ndende zao; ndipo Aisraele adzalamulira owavuta. Ndipo padzakhala tsiku loti Yehova adzakupumitsa chisoni chako, ndi nsautso yako, ndi ntchito yako yovuta, imene anakugwiritsa, pamenepo udzaimbira mfumu ya ku Babiloni nyimbo iyi yanchinchi, ndi kuti, Wovuta wathadi? Mudzi wagolide wathadi! Yehova wathyola mkunkhu wa woipa, ndodo yachifumu ya wolamulira. Wokantha anthu mwaukali kuwakantha chikanthire, wolamulira amitundu mokwiya, angosautsidwa wopanda womlanditsa. Dziko lonse lapuma, lili duu; iwo ayamba kuimba nyimbo. Inde, milombwa ikondwera ndi iwe, ndi mikungudza ya Lebanoni, ndi kunena, Chigwetsere iwe pansi, palibe wokwera kudzatidula ife. Kunsi kwa manda kugwedezeka, chifukwa cha iwe, kukuchingamira podza pako; kukuutsira iwe mizimu, ngakhale onse akuluakulu a dziko lapansi; kukweza kuchokera m'mipando yao mafumu onse a amitundu. Onse adzavomera, nadzati kwa iwe, Kodi iwe wakhalanso wopanda mphamvu ngati ife? Kodi iwe wafanana nafe? Chifumu chako chatsitsidwa kunsi kumanda, ndi phokoso la mingoli yako; mphutsi zayalidwa pansi pa iwe, ndi mphukutu zakukuta. Wagwadi kuchokera kumwamba, iwe nthanda, mwana wa mbandakucha! Wagwetsedwa pansi, iwe wolefula amitundu! Ndipo iwe unati mumtima mwako, Ndidzakwera kumwamba, ndidzakweza mpando wanga wachifumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu; ndidzakhala pamwamba pa phiri la khamu, m'malekezero a kumpoto; ndidzakwera pamwamba pa mitambo, ndidzafanana ndi Wam'mwambamwamba. Koma udzatsitsidwa kunsi kumanda, ku malekezero a dzenje. Iwo amene akuona iwe adzayang'anitsitsa iwe, nadzalingalira za iwe, ndi kuti, Kodi uyu ndi munthu amene ananthunthumiritsa dziko lapansi, amene anagwedeza maufumu; amene anapululutsa dziko, napasula midzi yake, amene sanamasule ndende zake, zinke kwao? Mafumu onse a mitundu, onsewo agona m'ulemerero yense kunyumba kwake. Koma iwe watayidwa kunja kwa manda ako, ngati nthambi yonyansa, ngati chovala cha ophedwa, opyozedwa ndi lupanga, otsikira kumiyala ya dzenje, monga ngati mtembo wopondedwa ndi phazi. Iwe sudzaphatikizidwa pamodzi nao poikidwa, pakuti iwe waononga dziko lako, wapha anthu ako; mbeu ya ochita zoipa sidzatchulidwa konse. Konzani inu popherapo ana ake, chifukwa cha kuipa kwa atate ao; kuti iwo asadzuka ndi kukhala nalo dziko, ndi kudzaza dziko lapansi ndi midzi. Ndipo Ine ndidzawaukira, ati Yehova wa makamu, ndi kuononga ku Babiloni dzina ndi otsala, ndi mwana wamwamuna, ndi chidzukulu chachimuna, ati Yehova. Ndidzayesapo pokhala nungu, ndi maiwe a madzi; ndipo ndidzasesapo ndi tsache la chionongeko, ati Yehova wa makamu. Yehova wa makamu walumbira, nati, Ndithu monga ndaganiza, chotero chidzachitidwa; ndipo monga ndapanga uphungu, chotero chidzakhala; kuti Ine ndidzathyola Asiriya m'dziko langa, ndi pamwamba pa mapiri anga ndidzawapondereza; pomwepo goli lake lidzachoka pa iwo, ndi katundu wake adzachoka paphuzi pao. Umenewu ndi uphungu wopangira dziko lonse; ndipo ili ndi dzanja lotambasulidwa pa amitundu onse. Pakuti Yehova wa makamu wapanga uphungu, ndani adzauleketsa? Ndi dzanja lake latambasulidwa, ndani adzalibweza? Chaka chimene mfumu Ahazi anamwalira katundu amene analipo. Usakondwere, iwe Filistiya, wonsewe, pothyoka ndodo inakumenya; pakuti m'muzu wa njoka mudzatuluka mphiri, ndimo chipatso chake chidzakhala njoka yamoto youluka. Ndi oyamba kubadwa a osauka adzadya, aumphawi nadzagona pansi osatekeseka; ndipo ndidzapha muzu wako ndi njala, ndi otsala ako adzaphedwa. Lira, chipata iwe; fuula, mudzi iwe; wasungunuka, Filistiya wonsewe, pakuti utsi uchokera kumpoto, ndipo palibe wosokera m'mizere yake. Ndipo adzayankhanji amithenga a amitundu? Kuti Yehova wakhazikitsa Ziyoni, ndipo m'menemo anthu ake ovutidwa adzaona pobisalira. Katundu wa Mowabu. Pakuti usiku umodzi Ari wa ku Mowabu wapasuka, nakhala chabe; usiku umodzi Kiri wa Mowabu wapasuka, nakhala chabe. Akwera ku Kachisi, ndi ku Diboni, kumisanje, kukalira; pa Nebo ndi pa Medeba a Mowabu pali kulira; pamitu pao ponse pali dazi, ndevu zonse zametedwa. M'makwalala mwao adzimangira chiguduli m'chuuno, pamwamba pa nyumba zao, ndi m'malo a mabwalo ao, yense akuwa, naliritsa kwambiri. Ndi Hesiboni afuula zolimba, ndi Eleyale; mau ao amveka, ngakhale ku Yahazi; chifukwa chake amuna ankhondo a Mowabu afuula zolimba; moyo wake wanthunthumira m'kati mwake. Mtima wanga ufuula chifukwa cha Mowabu: akulu ake athawira ku Zowari, ku Egilati-Selisiya; pakuti pa chikweza cha Luhiti akwera alikulira, pakuti m'njira ya Horonaimu akweza mfuu wa chionongeko. Pakuti pa madzi a Nimurimu padzakhala mabwinja; popeza udzu wafota, msipu watha. Chifukwa chake zochuluka adazipeza, ndi zosungidwa zao adzazitenga kunka nazo kumtsinje wa mabango. Pakuti kulira kwamveka kuzungulira malire a Mowabu; kukuwa kwake kwafikira ku Egilaimu, ndi kukuwa kwake kwafikira ku Beerelimu. Pakuti madzi a Diboni adzala mwazi; pakuti ndidzatengera zina pa Diboni, mkango pa iye amene anapulumuka ku Mowabu, ndi pa otsala a m'dziko. Tumizani inu anaankhosa kwa wolamulira wa dziko kuchokera ku Sela kunka kuchipululu, mpaka kuphiri la mwana wamkazi wa Ziyoni. Pakuti ana akazi a Mowabu adzakhala pa madooko a Arinoni, ngati mbalame zoyendayenda, ngati chisa chofwanchuka. Chitani uphungu, weruzani chiweruziro; yesa mthunzi wako monga usiku pakati pa usana; bisa opirikitsidwa, osawulula woyendayenda. Opirikitsidwa a Mowabu akhale ndi iwe, khala iwe chomphimba pamaso pa wofunkha; pakuti kumpambapamba kwalekeka, kufunkha kwatha, opondereza atsirizika m'dziko. Ndipo mpando wachifumu udzakhazikika m'chifundo, ndimo wina adzakhala pamenepo m'zoona, m'chihema cha Davide, nadzaweruza, nadzafunitsa chiweruziro, nadzafulumira kuchita chilungamo. Ife tinamva kunyada kwa Mowabu, kuti iye ali wonyada ndithu; ngakhale kudzitama kwake, ndi kunyada kwake ndi mkwiyo wake; matukutuku ake ali achabe. Chifukwa chake Mowabu adzakuwa chifukwa cha Mowabu, onse adzakuwa; chifukwa cha maziko a Kiri-Haresefi mudzalira maliro, osautsidwa ndithu. Pakuti minda ya ku Hesiboni yalefuka, ndi mpesa wa ku Sibima; ambuye a mitundu athyolathyola mitengo yosankhika yake; iwo anafikira ngakhale ku Yazere, nayendayenda m'chipululu; nthambi zake zinatasa, zinapitirira panyanja. Chifukwa chake ndidzalira ndi kulira kwa Yazere, chifukwa cha mpesa wa Sibima, ndidzakukhathamiza ndi misozi yanga, iwe Hesiboni ndi Eleyale; chifukwa kuti pa zipatso zako za malimwe, ndi pa masika ako, mfuu wankhondo wagwera. Ndipo chikondwero ndi msangalalo zachotsedwa m'munda wopatsa zipatso; ndi m'minda ya mipesa simudzakhala kuimba, ngakhale phokoso losangalala; palibe woponda adzaponda vinyo m'moponderamo; ndaleketsa mfuu wa masika amphesa. Chifukwa chake m'mimba mwanga mulirira Mowabu, ngati mngoli, ndi za m'mtima mwanga zilirira Kiriheresi. Ndipo padzakhala kuti pamene Mowabu adzadzionetsa yekha, ndi kudzitopetsa pamsanje, ndipo kufika kumalo ake oyera kudzapemphera, sadzapindulapo kanthu. Awa ndi mau amene Yehova adanena za Mowabu nthawi zapitazo. Koma tsopano Yehova wanena, nati, Zisanapite zaka zitatu monga zaka za wolembedwa ntchito, ulemerero wa Mowabu udzakhala wonyozeka, ndi khamu lalikulu lake, ndi otsala adzakhala ang'onong'ono ndi achabe. Katundu wa Damasiko. Taonani, Damasiko wachotsedwa usakhalenso mudzi, ndimo udzangokhala muunda wopasudwa. Midzi ya Aroere yasiyidwa; idzakhala ya zoweta zogona pansi, opanda woziopsa. Ku Efuremu sikudzakhalanso linga, ngakhale ufumu ku Damasiko, ngakhale otsala kwa Aramu; iwo adzakhala ngati ulemerero wa ana a Israele, ati Yehova wa makamu. Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti ulemerero wa Yakobo udzakhala wopyapyala, ndi kunenepa kwa thupi lake kudzaonda. Ndipo padzakhala ngati wamasika alikumweta tirigu wosacheka, ndi dzanja lake lilikudula ngala; inde padzakhala ngati pamene wina akunkha ngala m'chigwa cha Refaimu. Koma mudzasiyidwa m'menemo khunkha, monga ngati kugwedeza kwake kwa mtengo wa azitona, zipatso ziwiri pena zitatu m'nsonga ya nthambi yosomphoka, zinai pena zisanu m'nthambi za kunthemba, za mtengo wobalitsa, ati Yehova, Mulungu wa Israele. Tsiku limenelo munthu adzayang'ana kwa Mlengi wake, ndipo maso ake adzalemekeza Woyera wa Israele. Ndipo iye sadzayang'ana pa maguwa a nsembe, ntchito ya manja ake, ngakhale kulemekeza chimene anachipanga ndi zala zake, ngakhale zifanizo pena mafano a dzuwa. Tsiku limenelo midzi yake yolimba idzakhala ngati mabwinja a m'nkhalango, ndi a pansonga pa phiri, osiyidwa pamaso pa ana a Israele; ndipo padzakhala bwinja. Chifukwa iwe waiwala Mulungu wa chipulumutso chako, sunakumbukira thanthwe la mphamvu zako; chifukwa chake iwe waoka mitengo yokondweretsa, waokapo zipinjiri zachilendo; tsiku lako looka uzingapo mpanda, nuphukitsa mbeu zako m'mawa mwake; mulu wa masika udzaoneka tsiku lakulira ndi la chisoni chothetsa nzeru. Ha, phokoso la mitundu yambiri ya anthu ambiri, amene afuula ngati kukukuma kwa nyanja; ndi kuthamanga kwa amitundu, akuthamanga ngati kuthamanga kwa madzi amphamvu! Mitundu ya anthu idzathamanga ngati kuthamanga kwa madzi ambirimbiri; koma Iye adzawadzudzula, ndipo iwo adzathawira patali, nadzapirikitsidwa monga mankhusu a pamapiri patsogolo pa mphepo, ndi monga fumbi lokwetera patsogolo pa mkuntho wa mphepo. Pa nthawi ya madzulo, taonani kuopsa; kusanake, iwo palibe. Ili ndi gawo la iwo amene atifunkha ndi ichi chiwagwera omwe alanda zathu. Ha, dziko lakukupuza mapiko, lili tsidya lija la nyanja za Etiopiya; limene litumiza mithenga panyanja m'ngalawa zamagumbwa zoyenda m'madzi, ndi kuti, Mukani, inu mithenga yoyenda msangamsanga kumtundu wa anthu aatali ndi osalala, kwa mtundu woopsa chikhalire chao, mtundu umene uyesa dziko ndi kupondereza pansi, umene dziko lake nyanja ziligawa! Inu nonse akukhala m'dziko lapansi, ndi inu akukhazikika pa dziko lapansi, potukulidwa chizindikiro pamwamba pa mapiri, mudzaona, ndi polizidwa lipenga mudzamva. Pakuti Yehova watero kwa ine, Ine ndidzakhala chete, ndipo ndidzayang'ana mokhala chete, ndipo ndidzayang'ana mokhalamo Ine, monga kuwala kotentha kwa dzuwa, monga mtambo wa mame m'kutentha kwa masika. Pakuti masika asanafike, kutatha kuphuka ndi posanduka duwa mphesa yofuna kutcha, iye adzadzombolera tinthambi ndi chikwakwa, ndi nthambi zotasa adzazichotsa ndi kuzisadza. Adzasiyira mbalame zakulusa za m'mapiri ndi zilombo za dziko nthambizo, ndipo mbalame zakulusa zidzakhalapo m'dzinja, ndi zilombo zonse za dziko zidzakhalapo m'malimwe. Nthawi imeneyo mphatso idzaperekedwa kwa Yehova wa makamu, mtundu wa anthu aatali ndi osalala, yochokera kwa mtundu woopsa chikhalire chao; mtundu umene uyesa dziko ndi kupondereza pansi, umene dziko lake nyanja ziligawa, kumalo a dzina la Yehova wa makamu, phiri la Ziyoni. Katundu wa Ejipito. Taonani, Yehova wakwera pamwamba pa mtambo wothamanga, nadza ku Ejipito; ndi mafano a Ejipito adzagwedezeka pakufika kwake, ndi mtima wa Ejipito udzasungunuka pakati pake. Ndipo ndidzapikisanitsa Aejipito; ndipo adzamenyana wina ndi mbale wake, ndi wina ndi mnansi wake; mudzi kumenyana ndi mudzi, ndi ufumu kumenyana ndi ufumu. Ndipo mzimu wa Ejipito adzakhala wachabe pakati pake; ndipo Ine ndidzaononga uphungu wake; ndimo iwo adzafunafuna mafano ndi anyanga, ndi alauli, ndi obwebweta. Ndipo ndidzapereka Ejipito m'manja mwa mbuye wankharwe; ndi mfumu yaukali idzawalamulira, ati Ambuye, Yehova wa makamu. Ndipo madzi adzaphwa m'nyanja yaikulu, ndipo nyanja yoyendamo madzi idzaphwa, niuma. Ndipo nyanja zidzanunkha; mitsinje ya Ejipito idzachepa, nuima; bango ndi mlulu zidzafota. Madambo oyandikana ndi Nailo, pafupi ndi gombe la Nailo, ndi zonse zobzala pa Nailo zidzauma, nizichotsedwa, zosakhalanso konse. Asodzinso adzalira, ndi onse oponya mbedza m'Nailo adzaliralira, ndi onse oponya makoka m'madzi, adzalefuka. Komanso iwo amene agwira ntchito yakupala thonje, ndi iwo amene aomba nsalu yoyera, adzakhala ndi manyazi. Ndipo maziko ake adzasweka, onse amene agwira ntchito yolipidwa adzavutidwa mtima. Akalonga a Zowani apusa ndithu; uphungu wa aphungu anzeru a Farao wasanduka wopulukira; bwanji iwe unena kwa Farao, Ine ndine mwana wa anzeru, mwana wa mafumu akale? Nanga tsopano anzeru ali kuti? Akuuze iwe tsopano; adziwe chimene Yehova wa makamu watsimikiza mtima kuchitira Ejipito. Akalonga a Zowani apusa, akalonga a Nofi anyengedwa; iwo asocheretsa Ejipito, amene ali mwala wa pangodya wa mafuko ake. Yehova wasanganiza mzimu wa kusaweruzika pakati pake; ndipo iwo asocheretsa Ejipito m'ntchito zake zonse, monga mwamuna woledzera ayenda punzipunzi posanza pake. Ejipito sadzakhala ndi ntchito, imene mutu pena mchira, pena nthambi ya kanjedza, pena mlulu zidzaigwira. Tsiku limenelo Ejipito adzanga akazi; ndipo adzanthunthumira ndi kuopa, chifukwa cha kugwedeza kwa dzanja la Yehova wa makamu, limene Iye agwedeza pamwamba pake. Ndipo dziko la Yuda lidzaopsa Ejipito, yense wakulitchula adzamtembenukira mwamantha, chifukwa cha uphungu wa Yehova wa makamu, aupanga pa dzikolo. Tsiku limenelo padzakhala midzi isanu m'dziko la Ejipito yolankhula chinenero cha Kanani, ndi yolumbira, Pali Yehova wa makamu; wina udzatchedwa, Mudzi wa chionongeko. Tsiku limenelo padzakhala guwa la nsembe la Yehova pakati pa dziko la Ejipito, ndi choimiritsa cha Yehova m'malire ake. Ndipo chidzakhala chizindikiro ndi mboni ya Yehova wa makamu m'dziko la Ejipito; pakuti iwo adzalirira kwa Yehova, chifukwa cha osautsa, ndipo Iye adzawatumizira mpulumutsi, ndi wamphamvu, nadzawapulumutsa. Ndipo Yehova adzadziwika kwa Ejipito, ndipo Aejipito adzadziwa Yehova tsiku limenelo; inde iwo adzapembedzera ndi nsembe ndi zopereka, nadzawindira Yehova ndi kuchitadi. Ndipo Yehova adzakantha Ejipito kukantha ndi kuchiritsa; ndipo iwo adzabwerera kwa Yehova, ndipo Iye adzapembedzedwa ndi iwo, nadzawachiritsa. Tsiku limenelo padzakhala khwalala lochokera m'Ejipito kunka ku Asiriya, ndipo Mwasuri adzafika ku Ejipito, ndi Mwejipito adzafika ku Asiriya, ndipo Aejipito adzapembedzera pamodzi ndi Aasiriya. Tsiku limenelo Israele ndi Ejipito ndi Asiriya atatuwa, adzakhala mdalitso pakati pa dziko lapansi; pakuti Yehova wa makamu wadalitsa iwo, ndi kuti, Odalitsika Ejipito anthu anga, ndi Asiriya ntchito ya manja anga, ndi Israele cholowa changa. Chaka chimene kazembe wa ku Asiriya anafika ku Asidodi, muja Sarigoni mfumu ya Asiriya anamtumiza iye, ndipo iye anamenyana ndi Asidodi, naugonjetsa. Nthawi imeneyo Yehova ananena ndi Yesaya, mwana wa Amozi, nati, Muka numasule chiguduli m'chuuno mwako, nuchichotse, nuvule nsapato yako kuphazi lako. Ndipo iye anatero, nayenda maliseche, ndi wopanda nsapato. Ndipo Yehova anati, Monga mtumiki wanga Yesaya wayenda maliseche ndi wopanda nsapato zaka zitatu, akhale chizindikiro ndi chodabwitsa kwa Ejipito ndi kwa Etiopiya; momwemo mfumu ya Asiriya idzatsogolera kwina am'nsinga a Ejipito, ndi opirikitsidwa a Etiopiya, ana ndi okalamba, amaliseche ndi opanda nsapato, ndi matako osavala, kuti achititse manyazi Ejipito. Ndipo iwo adzakhala ndi mantha ndi manyazi, chifukwa cha Kusi, amene anawatama, ndi Ejipito, amene anawanyadira. Ndipo wokhala m'mphepete mwa nyanja muno adzati tsiku limenelo, Taonani, kuyembekeza kwathu kuli kotero, kumene ife tinathawira atithangate kupulumutsidwa kwa mfumu ya Asiriya, ndipo ife tidzapulumuka bwanji? Katundu wa chipululu cha kunyanja. Monga akamvulumvulu a kumwera apitirira, kufumira kuchipululu kudziko loopsa. Masomphenya ovuta aonetsedwa kwa ine; wogula malonda wonyenga amangonyenga, ndi wofunkha amangofunkha. Kwera Elamu iwe; zunguniza Mediya iwe; kuusa moyo kwake konse ndakutonthoza. Chifukwa chake m'chuuno mwanga mwadzazidwa ndi zopota; zopweteka zandigwira ine monga zopweteka za mkazi pobala mwana; zowawa zindiweramitsa, makutu anga sangathe kumva; ndichita mantha sindingathe kuona. Mtima wanga uguguda, mantha andiopsetsa ine; chizirezire chimene ndinachikhumba chandisandukira kunthunthumira. Iwo akonza pa gome lodyera, aika alonda, adya, namwa; ukani, akalonga inu, dzozani mafuta chikopa. Pakuti Ambuye atero kwa ine, Muka, ika mlonda anene chimene achiona; ndipo pamene iye anaona khamu, amuna apakavalo awiriawiri, khamu la abulu, khamu la ngamira, iye adzamvetsera ndi khama mosamalitsa. Ndipo iye anafuulitsa ngati mkango, Ambuye inu, ine ndiimabe pamwamba pa nsanja nthawi ya usana, ndipo ndiikidwa mu ulonda wanga usiku wonse; ndipo taonani, kuno kulinkudza khamu la amuna, apakavalo awiriawiri. Ndipo iye anayankha nati, Babiloni wagwa, wagwa; ndi mafano onse osema a milungu yake asweka, nagwa pansi. Kuomba kwanga nanga, ndi za pa dwale langa: chimene ine ndinachimva kwa Yehova wa makamu Mulungu wa Israele, ndanena kwa inu. Katundu wa Duma. Wina aitana kwa ine kuchokera ku Seiri, Mlonda, nthawi yanji ya usiku? Mlonda, nthawi yanji ya usiku? Mlonda anati, Kuli kucha, koma kukali usiku; mukafuna kufunsa, funsani, bwerani, idzani. Katundu wa pa Arabiya. M'nkhalango ya m'Arabiya mudzagona, inu makamu oyendayenda a Dedani. Muchingamire akumva ludzu ndi madzi; okhala m'dziko la Tema ananka kukomana ndi othawa ndi chakudya chao. Pakuti iwo anathawa malupanga, malupanga osololedwa, ndi mauta olifuka ndi nkhondo yovuta. Pakuti Ambuye anatero kwa ine, Chisanapite chaka malinga ndi zaka za wolembedwa ntchito, ulemerero wonse wa Kedara udzagoma; ndi otsala amauta, ngwazi za ana a Kedara zidzachepa, pakuti Yehova Mulungu wa Israele wanena. Katundu wa chigwa cha masomphenya. Mwatani kuti mwakwera nonsenu pamachindwi? Iwe amene wadzala ndi zimfuu, mudzi waphokoso, mudzi wokondwa; ophedwa ako sanaphedwe ndi lupanga, sanafe m'nkhondo. Olamulira ako onse athawa pamodzi, anamangidwa ndi amauta; opezedwa ako onse anamangidwa pamodzi, nathawira patali. Chomwecho ndinati, Usandiyang'ane ine, ndilira ndi kuwawa mtima; usafulumire kunditonthoza ine, chifukwa cha kufunkhidwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga. Pakuti nditsiku laphokoso, ndi lopondereza pansi, ndi lothetsa nzeru, lochokera kwa Ambuye Yehova wa makamu, m'chigwa cha masomphenya, kugumuka kwa malinga, ndi kufuulira kumapiri. Ndipo Elamu anatenga phodo, ndi magaleta a anthu ndi apakavalo; ndipo Kiri anaonetsa zikopa. Ndipo panali kuti zigwa zako zosankhika zinadzala magaleta, ndi apakavalo anadzinika okha pachipata. Ndipo Iye anachotsa chophimba cha Yuda; ndipo iwe unayang'ana tsiku limenelo pa zida za m'nyumba ya nkhalango. Ndipo inu munaona kuti pa mudzi wa Davide panagumuka mipata yambiri; ndipo munasonkhanitsa pamodzi madzi a m'thamanda lakunsi. Ndipo inu munawerenga nyumba za Yerusalemu, ndipo munagwetsa nyumba, kuti mumangire linga. Inu munapanganso chosungamo madzi a thamanda lakale, pakati pa malinga awiri; koma inu simunamuyang'ane iye amene anachichita icho, ngakhale kusamalira iye amene analipanga kale. Ndipo tsiku limenelo Ambuye, Yehova wa makamu, anaitana kulira, ndi kugwa misozi, ndi kumeta, ndi kuvala chiguduli m'chuuno; koma taonani, kukondwa, ndi kusekerera, ndi kupha ng'ombe, ndi kupha nkhosa, ndi kudya nyama, ndi kumwa vinyo; tiyeni tidye ndi kumwa, chifukwa mawa tidzafa. Ndipo Yehova wa makamu wadzivumbulutsa yekha m'makutu mwanga, Ndithu choipa chimenechi sichidzachotsedwa pa inu kufikira inu mudzafa, ati Ambuye, Yehova wa makamu. Atero Ambuye Yehova wa makamu, Muka, pita iwe kwa kapitao uyu, kwa Sebina woyang'anira nyumba, ndi kuti, Uchitanji iwe kuno, ndimo ndani ali nawe kuno, kuti iwe wagoba manda kuno, ndi kudzigobera manda pamwamba, ndi kudzisemera mogonamo m'thanthwe. Taona Yehova adzakuponya iwe zolimba, monga mwamuna wamphamvu, inde adzakufumbata zolimba. Iye ndithu adzakuzunguza, ndi kukuponyaponya ngati mpira m'dziko lalikulu; kumeneko iwe udzafa, ndipo kumeneko kudzakhala magaleta a ulemerero wako, iwe wochititsa manyazi banja la mbuye wako. Ndipo Ine ndidzakutulutsa iwe mu ntchito yako, ndi kukutsitsa iwe pokhala pako. Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti Ine ndidzaitana mtumiki wanga, Eliyakimu mwana wa Hilikiya: ndipo ndidzamveka iye chovala chako, ndi kumlimbikitsa ndi lamba lako, ndipo ndidzapereka ulamuliro wako m'dzanja lake; ndipo iye adzakhala atate wa okhala m'Yerusalemu ndi a nyumba ya Yuda. Ndipo ndidzaika mfungulo wa nyumba ya Davide paphewa pake, ndipo iye adzatsegula, ndipo palibe wina adzatseka, iye adzatseka ndipo palibe wina adzatsegula. Ndipo ndidzamkhomera iye ngati chikhomo cholimba; ndipo iye adzakhala mpando wa ulemerero wa banja la atate wake. Ndipo iwo adzapachika pa iye ulemerero wonse wa banja la atate wake, obadwa ndi ana, mbiya zonse zazing'ono, ngakhale zikho ndi aguda omwe. Tsiku limenelo, ati Yehova wa makamu, chikhomo chokhomeredwa polimba udzasukusika; nudzaguluka, ndi kugwa, ndi katundu wopachikidwapo adzadulidwa; pakuti Yehova wanena. Katundu wa Tiro. Kuwani, inu ngalawa za Tarisisi; chifukwa wapasudwa, kulibenso nyumba, kulibe polowera; kuchokera kudziko la Kitimu kwavumbulutsidwa kwa iwo. Khalani chete, inu okhala m'chisumbu; iwe amene anakudzazanso amalonda a ku Sidoni, opita m'nyanja. Ndi pa nyanja zazikulu anapindula ndi mbeu za ku Sihori ndizo dzinthu za ku Nailo; ndi kumeneko kunali msika wa amitundu. Khala ndi manyazi, iwe Sidoni; chifukwa nyanja yanena, linga la kunyanja, ndi kuti, Ine sindinamve zowawa, kapena kubala, kapena kulera anyamata, kapena kulera anamwali. Pofika mbiriyo ku Ejipito, iwo adzamva kuwawa kwambiri pa mbiri ya Tiro. Olokani inu, kunka ku Tarisisi, kuwani, inu okhala m'chisumbu. Kodi umene ndi mudzi wanu wokondwa, wachikhalire kale lomwe, umene mapazi ake anaunyamula kunka nao kutali kukhalako? Ndani wapanga uphungu uno pa Tiro, mudzi umene upereka akorona, amalonda ake ali akalonga, ogulitsa ake ali olemekezeka pa dziko lapansi? Yehova wa makamu wapanga uphungu uwu, kuipitsa kunyada kwa ulemerero wonse, kupepula onse olemekezeka a m'dziko lapansi. Pita pakati pa dziko lako monga Nailo, iwe mwana wamkazi wa Tarisisi; palibenso lamba. Iye watambasula dzanja lake panyanja, wagwedeza maufumu; Yehova walamulira Kanani za amalonda, kupasula malinga ake. Ndipo Iye anati, Iwe sudzakondwanso konse, iwe namwali wovutidwa, mwanawamkazi wa Sidoni; uka, oloka kunka ku Kitimu; ngakhale kumeneko iwe sudzapumai. Taonani, dziko la Ababiloni; anthu awa sakhalanso; Asiriya analiika ilo likhale la zilombo zokhala m'chipululu; iwo amanga nsanja zao, nagumula nyumba za mafumu ake; nalipasula. Kuwani, inu ngalawa za Tarisisi; pakuti linga lanu lapasulidwa. Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti Tiro adzaiwalika zaka makumi asanu ndi awiri, malinga ndi masiku a mfumu imodzi; zitapita zaka makumi asanu ndi ziwirizo, chidzakhala kwa Tiro monga m'nyimbo ya mkazi wadama. Tenga mngoli, yendayenda m'mudzi, iwe mkazi wadama, amene unaiwalika; imba zokoma, chulukitsa nyimbo, kuti ukumbukiridwe. Ndipo padzali, zitapita zaka makumi asanu ndi awirizo, kuti Yehova adzazonda Tiro, ndipo iye adzabwerera kumphotho yake, nadzachita dama ndi maufumu onse a dziko lapansi, okhala kunja kuno. Malonda ake ndi mphotho yake zidzakhala zopatulikira Yehova; sizidzasungidwa kapena kuikidwa; chifukwa malonda ake adzakhala kwa iwo, amene akhala pamaso pa Yehova, kuti adye mokwana, navale chaulemu. Taonani, Yehova apululutsa dziko, nalipasula, nalitembenuza dodolido, nabalalitsa okhalamo ake. Ndipo padzakhala monga ndi anthu, moteronso ndi ansembe; monga ndi mtumiki, moteronso ndi mbuyake; monga ndi mdzakazi, moteronso ndi mbuyake wamkazi; monga ndi wogula, moteronso ndi wogulitsa; monga ndi wobwereka, moteronso ndi wombwereka; monga ndi wotenga phindu, moteronso ndi wombwezera phindu kwa iye. Dziko lidzapululuka konse, ndi kupasulidwa ndithu; pakuti Yehova anenana mau amenewa. Dziko lirira nilifota, dziko lilefuka nilifota, anthu omveka a padziko alefuka. Dzikonso laipitsidwa ndi okhalamo ake omwe, chifukwa iwo alakwa pamalamulo nasinthanitsa malemba, nathyola chipangano cha nthawi zonse. Chifukwa chake chitemberero chadya dziko, ndi amene akhala m'menemo apezedwa ochimwa, chifukwa chake okhalamo a padziko atenthedwa, ndipo anthu owerengeka atsala. Vinyo watsopano alira, mpesa ulefuka, mitima yonse yokondwa iusa moyo. Kusangalala kwa mangaka kwalekeka, phokoso la iwo amene asekera litha, kukondwa kwa mngoli kwalekeka. Iwo sadzamwa vinyo ndi kuimba nyimbo; chakumwa chaukali chidzawawa kwa iwo amene achimwa. Mudzi wosokonezeka wagwetsedwa pansi; nyumba zonse zatsekedwa, kuti asalowemo munthu. Muli mfuu m'makwalala chifukwa cha vinyo; kukondwa konse kwadetsedwa, kusangalala kwa dziko kwatha. M'mudzi mwatsala bwinja, ndi chipata chamenyedwa ndi chipasuko. Chifukwa chake padzakhala chotero pakati pa dziko mwa anthu, ngati kugwedeza kwa mtengo wa azitona, ngati khunkha la mphesa, pakutha masika ake. Amenewa adzakweza mau ao, nadzafuula; chifukwa cha chifumu cha Yehova, iwo adzafuula zolimba panyanja. Chifukwa chake lemekezani inu Yehova kum'mawa, ngakhale dzina la Yehova, Mulungu wa Israele, m'zisumbu za m'nyanja. Kuchokera ku malekezero a dziko ife tamva nyimbo zolemekeza wolungama. Koma ine ndinati, Ndaonda ine, ndaonda ine, tsoka kwa Ine! Amalonda onyenga amangonyenga; inde ogulitsa onyenga apambana kunyenga. Mantha ndi dzenje ndi msampha zili pa iwe, wokhala m'dziko. Ndipo padzali, kuti iye amene athawa mbiri yoopsa, adzagwa m'dzenje; ndi iye amene atuluka m'kati mwa dzenje, adzakodwa mumsampha, pakuti mazenera a kuthambo atsegudwa, ndi maziko a dziko agwedezeka. Dziko lapansi lasweka ndithu, dziko lapansi lasungunukadi, dziko lapansi lili kugwedezeka kopambana. Dziko lapansi lidzachita dzandidzandi, ngati munthu woledzera, ndi kunjenjemera, ngati chilindo; ndi kulakwa kwake kudzalilemera, ndipo lidzagwa losaukanso. Ndipo padzali tsiku limenelo, kuti Yehova adzazonda kumwamba khamu lakumwamba, ndi mafumu a dziko lapansi. Ndipo iwo adzasonkhanitsidwa pamodzi, monga ndende zimasonkhanitsidwa m'dzenje, ndi kutsekeredwa m'kaidi, ndipo atapita masiku ambiri adzawazonda. Pompo mwezi udzanyazitsidwa, ndi dzuwa lidzakhala ndi manyazi, pakuti Yehova wa makamu adzalamulira chaulemerero m'phiri la Ziyoni, ndi m'Yerusalemu, ndi pamaso pa akuluakulu ake. Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga, ndidzakukuzani Inu, ndidzatamanda dzina lanu, chifukwa mwachita zinthu zodabwitsa, ngakhale zauphungu zakale, mokhulupirika ndi m'zoonadi. Chifukwa Inu mwasandutsa mudzi muunda; mudzi walinga bwinja; nyumba ya alendo kuti isakhale mudzi; sudzamangidwa konse. Chifukwa chake anthu amphamvu adzakulemekezani Inu, mudzi wa mitundu yakuopsa udzakuopani Inu. Chifukwa Inu mwakhala linga la aumphawi, linga la osowa m'kuvutidwa kwake, pobisalira chimphepo, mthunzi wa pa dzuwa, pamene kuomba kwa akuopsa kufanana ndi chimphepo chakuomba tchemba. Monga kutentha m'malo ouma, Inu mudzaletsa phokoso la alendo; nyimbo ya akuopsa idzaletseka, monga mthunzi uletsa dzuwa. Ndipo m'phiri limeneli Yehova wa makamu adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okhaokha, la vinyo wansenga wokuntha bwino. Ndipo Iye adzaononga m'phiri limeneli chophimba nkhope chovundikira mitundu yonse ya anthu, ndi nsalu yokuta amitundu onse. Iye wameza imfa kunthawi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse; ndipo chitonzo cha anthu ake adzachichotsa pa dziko lonse lapansi; chifukwa Yehova wanena. Ndipo adzanena tsiku limenelo, Taonani, uyu ndiye Mulungu wathu; tamlindirira Iye, adzatipulumutsa; uyu ndiye Yehova, tamlindirira Iye, tidzakondwa ndi kusekerera m'chipulumutso chake. Chifukwa m'phiri limeneli dzanja la Yehova lidzakhalamo, ndipo Mowabu adzaponderezedwa pansi m'malo ake, monga udzu aponderezedwa padzala. Ndipo iye adzatambasula manja ake pakati pamenepo, monga wosambira atambasula manja ake posambira; koma Iye adzagwetsa pansi kunyada kwake, pamodzi ndi kunyenga kwa manja ake. Ndipo linga la pamsanje la machemba ako Iye waligwetsa, naligonetsa pansi, nalifikitsa padothi, ngakhale pafumbi. Tsiku limenelo adzaimba nyimbo imeneyi m'dziko la Yuda, Ife tili ndi mudzi wolimba; Iye adzaika chipulumutso chikhale machemba ndi malinga. Tsegulani pazipata, kuti mtundu wolungama, umene uchita zoonadi, ulowemo. Inu mudzasunga mtima wokhazikika mu mtendere weniweni, chifukwa ukukhulupirirani Inu. Khulupirirani Yehova nthawi yamuyaya, pakuti mwa Ambuye Yehova muli thanthwe lachikhalire. Chifukwa Iye watsitsira pansi iwo amene anakhala pamwamba, mudzi wa pamsanje; Iye wautsitsa, wautsitsira pansi; waugwetsa pansi pa fumbi. Phazi lidzaupondereza pansi; ngakhale mapazi a aumphawi, ndi mapondedwe a osowa. Njira ya wolungama ili njira yoongoka; Inu amene muli woongoka, mukonza njira ya wolungama. Inde m'njira ya maweruziro anu, Yehova, ife talindira Inu; moyo wathu ukhumba dzina lanu, ndi chikumbukiro chanu. Ndi moyo wanga ndinakhumba Inu usiku; inde ndi mzimu wanga wa mwa ine ndidzafuna Inu mwakhama; pakuti pamene maweruziro anu ali pa dziko lapansi, okhala m'dziko lapansi adzaphunzira chilungamo. Ungayanje woipa, koma sadzaphunzira chilungamo; m'dziko la machitidwe oongoka, iye adzangochimwa, sadzaona chifumu cha Yehova. Yehova, dzanja lanu litukulidwa, koma iwo saona; koma iwo adzaona changu chanu cha kwa anthu, nadzakhala ndi manyazi; inde moto udzamaliza adani anu. Yehova, mudzatikhazikitsira mtendere; pakuti mwatigwirira ntchito zathu zonse. Yehova Mulungu wathu, pamodzi ndi Inu Ambuye ena adatilamulira ife; koma mwa Inu nokha tidzatchula dzina lanu. Iwo afa, atha, sadzakhalanso ndi moyo; ali mizimu, sadzauka; chifukwa chake Inu munawazonda, ndi kuwaononga, mwathetsa chikumbukiro chao chonse. Mwachulukitsa mtundu, Yehova, mwachulukitsa mtundu; Inu mwalemekezeka, mwakuza malire onse a dziko. Yehova, iwo adza kwa Inu movutika, iwo anathira pemphero, muja munalikuwalanga. Monga ngati mkazi wokhala ndi pakati, amene nthawi yake yakubala yayandikira, amva zopweteka, ndi kufuula m'zowawa zake; momwemo takhala ife pamaso panu, Yehova. Ife tinali ndi pakati, ife tinamva zopweteka, tafanana ngati tabala mphepo; sitinachite chipulumutso chilichonse pa dziko lapansi; ngakhale okhala m'dziko lapansi sanagwe. Akufa anu adzakhala ndi moyo; mitembo yao idzauka. Ukani muimbe, inu amene mukhala m'fumbi; chifukwa mame ako akunga mame a pamasamba, ndipo dziko lapansi lidzatulutsa mizimu. Idzani, anthu anga, lowani m'zipinda mwanu, nimutseke pamakomo panu; nimubisale kanthawi kufikira mkwiyo utapita. Pakuti taonani, Yehova adza kuchokera kumalo ake kudzazonda okhala pa dziko lapansi, chifukwa cha kuipa kwao; dziko lidzavumbulutsa mwazi wake, ndipo silidzavundikiranso ophedwa ake. Tsiku limenelo Yehova ndi lupanga lake lolimba ndi lalikulu ndi lamphamvu adzalanga Leviyatani njoka yothamanga, ndi Leviyatani njoka yopindikapindika; nadzapha ching'ona chimene chili m'nyanja. Tsiku limenelo: munda wa mphesa wavinyo, imbani inu za uwo. Ine Yehova ndiusunga uwo; ndidzauthirira madzi nthawi zonse; ndidzausunga usiku ndi usana, kuti angauipse. Ndilibe ukali; ndani adzalimbanitsa lunguzi ndi minga ndi Ine kunkhondo? Ndiziponde ndizitenthe pamodzi. Kapena mlekeni, agwire mphamvu zanga, nachite nane mtendere; inde, achite nane mtendere. M'mibadwo ikudzayo Yakobo adzamera mizu; Israele adzaphuka ndi kuchita mphundu; ndipo iwo adzadzaza ndi zipatso pa dziko lonse lapansi. Kodi Mulungu wakantha Yakobo, monga umo anawakanthira akumkanthawo? Kapena kodi iye waphedwa malinga ndi kuphedwa kwa iwo amene anaphedwa ndi iye? Munalimbana naye pang'ono, pamene munamchotsa; wamchotsa iye kuomba kwake kolimba tsiku la mphepo yamlumbanyanja. Chifukwa chake, mwa ichi choipa cha Yakobo chidzafafanizidwa, ndipo ichi ndi chipatso chonse chakuchotsa tchimo lake; pamene iye adzayesa miyala yonse ya guwa la nsembe, ngati miyala yanjeresa yoswekasweka, zifanizo ndi mafano a dzuwa sizidzaukanso konse. Pakuti mudzi wochingidwa uli pa wokha, mokhalamo mwa bwinja, ndi mosiyidwa ngati chipululu; mwanawang'ombe adzadya kumeneko, nadzagonako pansi, nadzamaliza nthambi zake. Ponyala nthambi zake zidzathyoledwa; akazi adzafika, nazitentha ndi moto, pakuti ali anthu opanda nzeru; chifukwa chake Iye amene anawalenga sadzawachitira chisoni, ndi Iye amene anawaumba sadzawakomera mtima. Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti Yehova adzaomba tirigu wake, kuchokera madzi a nyanja, kufikira kumtsinje wa Ejipito, ndipo mudzakunkhidwa mmodzi, inu ana a Israele. Ndipo padzakhala tsiku limenelo, lipenga lalikulu lidzaombedwa; ndipo adzafika omwe akadatayika m'dziko la Asiriya, ndi opirikitsidwa a m'dziko la Ejipito; ndipo adzapembedza Yehova m'phiri lopatulika la pa Yerusalemu. Tsoka kwa korona wakunyada wa oledzera a Efuremu, ndi kwa duwa lakufota la ulemerero wake wokongola, limene lili pamutu paiwo, amene agwidwa ndi vinyo, m'chigwa cha nthaka yabwino. Taonani, Ambuye ali ndi wina wamphamvu wolimba; ngati chimphepo cha matalala, mkuntho wakuononga, ngati namondwe wa madzi amphamvu osefukira, adzagwetsa pansi ndi dzanja lamphamvu. Korona wakunyada wa oledzera a Efuremu adzaponderezedwa; ndi duwa lakufota la ulemerero wake wokongola, limene lili pamutu pa chigwa cha nthaka yabwino, lidzakhala ngati nkhuyu yoyamba kucha malimwe asanafike; poiona wakupenya imeneyo, amaidya ili m'dzanja lake. Tsiku limenelo Yehova wa makamu adzakhala korona wa ulemerero, ndi korona wokongola kwa anthu ake otsala: ndipo adzakhala mzimu wa chiweruziro kwa oweruza milandu, ndi mphamvu kwa iwo amene abweza nkhondo pachipata. Koma iwonso adzandima ndi vinyo, nasochera ndi chakumwa chaukali, wansembe ndi mneneri adzandima ndi chakumwa chaukali, iwo amezedwa ndi vinyo, nasochera ndi chakumwa chaukali, adzandima popenya, naphunthwa poweruza. Pakuti magome onse adzazidwa ndi masanzi ndi udyo, palibe malo okonzeka. Kodi Mulungu adzaphunzitsa yani nzeru? Kodi Iye adzamvetsa yani uthengawo? Iwo amene aletsedwa kuyamwa, nachotsedwa pamawere? Pakuti pali langizo ndi langizo, langizo ndi langizo; lamulo ndi lamulo, lamulo ndi lamulo; kuno pang'ono, uko pang'ono. Iai, koma ndi anthu a milomo yachilendo, ndi a lilime lina, Iye adzalankhula kwa anthu awa; amene ananena nao, Uku ndi kupuma, mupumitsa wolema, ndi apa ndi potsitsimutsa, koma iwo anakana kumva. Chifukwa chake mau a Yehova adzakhala kwa iwo langizo ndi langizo, langizo ndi langizo; lamulo ndi lamulo, lamulo ndi lamulo; kuno pang'ono, uko pang'ono; kuti ayende ndi kugwa chambuyo, ndi kuthyoka, ndi kukodwa mumsampha, ndi kugwidwa. Chifukwa chake imvani mau a Yehova, inu amuna amnyozo, olamulira anthu awa a m'Yerusalemu. Chifukwa inu munati, Ife tapangana pangano ndi imfa, tavomerezana ndi kunsi kwa manda; pakuti mliri wosefukira sudzatifikira ife; pakuti tayesa mabodza pothawirapo pathu, ndi kubisala m'zonyenga; chifukwa chake Ambuye Yehova atero, Taonani, ndiika m'Ziyoni mwala wa maziko, mwala woyesedwa mwala wa pangodya, wa mtengo wake wokhazikika ndithu; wokhulupirira sadzafulumira. Ndipo ndidzayesa chiweruziro chingwe choongolera, ndi chilungamo chingwe cholungamitsira chilili; ndipo matalala adzachotsa pothawirapo mabodza, ndi madzi adzasefukira mobisalamo. Ndipo pangano lanu ndi imfa lidzathedwa, ndi kuvomerezana kwanu ndi kunsi kwa manda kudzalephereka; popita mliri woopsa udzakuponderezani pansi. Nthawi zonse umapita, udzakutengani; chifukwa m'mawa ndi m'mawa udzapita, usana ndi usiku; ndipo kudzakhala kuopsa kokha, kumva mbiri yake. Pakuti kama wafupika, munthu sangatambalale pamenepo; ndi chofunda chachepa, sichingamfikire. Pakuti Yehova adzauka monga m'phiri la Perazimu, nadzakwiya monga m'chigwa cha Gibiyoni; kuti agwire ntchito yake, ntchito yake yachilendo, ndi kuti achite chochita chake, chochita chake chachilendo. Tsono musakhale amnyozo, kuti nsinga zanu zingalimbe; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, wandimvetsa za chionongeko chotsimikizidwa pa dziko lonse lapansi. Tcherani inu makutu, imvani mau anga; mverani, imvani kulankhula kwanga. Kodi mlimi amalimabe kuti abzale? Kodi amachocholabe, ndi kuswa zibuma za nthaka? Atakonza thyathyathya pamwamba pake, kodi safesa ponse mawere, ndi kumwazamwaza chitowe, nafesa tirigu m'mizere ndi barele m'malo ake osankhika, ndi mchewere m'maliremo? Pakuti Mulungu wake amlangiza bwino namphunzitsa. Pakuti sapuntha mawere ndi chopunthira chakuthwa, ngakhale kuzunguniza njinga ya galeta pachitowe; koma amakulunga mawere ndi munsi, naomba chitowe ndi chibonga. Tirigu wa mkate aperedwa; pakuti samampuntha osaleka; ngakhale kuyendetsapo njinga ya galeta wake, ngakhale kumphwanya ndi ziboda za akavalo ake sapera. Ichinso chifumira kwa Yehova wa makamu, uphungu wake uzizwitsa ndi nzeru yake impambana. Eya Ariyele, Ariyele, mudzi umene Davide anamangapo zithando! Onjezerani chaka ndi chaka; maphwando afikenso; pamenepo ndidzasautsa Ariyele, ndipo padzakhala maliro ndi kulira; koma iye adzakhala kwa Ine monga Ariyele. Ndipo ndidzamanga zithando kuzungulira iwe ponse, ndipo ndidzamanga linga ndi kuunjika miulu yakumenyanirana ndi iwe. Ndipo iwe udzagwetsedwa pansi, nudzanena uli pansi, ndi kulankhula kwako kudzakhala pansi kotuluka m'fumbi; ndi mau ako adzakhala ngati a wina amene ali ndi mzimu wobwebweta, kuchokera pansi, ndi kulankhula kwako kudzakhala konong'ona kochokera m'fumbi. Koma khamu la achilendo ako lidzafanana ndi fumbi losalala, ndi khamu la oopsa lidzakhala monga mungu wochokachoka; inde kudzaoneka modzidzimuka dzidzidzi. Ndipo Yehova wa makamu adzamzonda ndi bingu, ndi chivomezi, ndi mkokomo waukulu, kamvulumvulu, ndi mkuntho, ndi lawi la moto wonyambita. Ndipo khamu la mitundu yonse yomenyana ndi Ariyele, ngakhale yonse yomenyana naye ndi linga lake, ndi kumsautsa idzafanana ndi loto, masomphenya a usiku. Ndipo kudzafanana ndi munthu wanjala, pamene alota, ndipo, taonani, akudya; koma auka, ndipo m'kati mwake muli zii; kapena monga munthu waludzu pamene alota, ndipo taonani, akumwa; koma auka ndipo taonani walefuka, ndipo m'kati mwake muli gwa; momwemo lidzakhala khamu la mitundu yonse yomenyana ndi phiri la Ziyoni. Khalani ndi kudabwa; sangalalani ndi kukhala akhungu; iwo aledzera, koma si ndi vinyo, ali dzandidzandi; koma si ndi chakumwa chaukali. Pakuti Yehova watsanulira pa inu mzimu wa tulo togonetsa, natseka maso anu, ndiwo aneneri; naphimba mitu yanu, ndiwo alauli. Ndipo masomphenya onse akusandukirani mau a m'buku limatidwa ndi phula, limene anthu amapereka kwa wina wodziwa kuwerenga, nati, Werengani umu; koma ati, Sindingathe, chifukwa lamatidwa ndi phula; ndipo buku laperekedwa kwa wosadziwa kuwerenga, ndi kuti, Werengani umu; koma ati, Ine sindinaphunzira. Ndipo Ambuye anati, Popeza anthu awa ayandikira ndi Ine ndi m'kamwa mwao, nandilemekeza ndi milomo yao, koma mtima wao uli kutali ndi Ine, ndi mantha ao akundiopa Ine, ndi lamulo la anthu analiphunzira; chifukwa chake, taonani, ndidzachitanso mwa anthu awa ntchito yodabwitsa, ngakhale ntchito yodabwitsa ndi yozizwitsa; ndipo nzeru ya anthu ao anzeru idzatha, ndi luntha la anthu ao ozindikira lidzabisika. Tsoka kwa iwo amene afunitsa kubisira Yehova uphungu wao, ndi ntchito zao zili mumdima, ndipo amati ndani ationa ife? Ndani atidziwa ife? Ozolitsa inu! Kodi woumba adzayesedwa ngati dothi; kodi chinthu chopangidwa chinganene za iye amene anachipanga, Iye sanandipange ine konse; kapena kodi chinthu choumbidwa chinganene za iye amene anachiumba, Iye alibe nzeru? Kodi sikatsala kamphindi kakang'ono, ndipo Lebanoni adzasanduka munda wobalitsa, ndi munda wobalitsa udzayesedwa nkhalango? Ndipo tsiku limenelo gonthi adzamva mau a m'buku, ndi maso akhungu adzaona potuluka m'zoziya ndi mumdima. Ofatsanso kukondwa kwao kudzachuluka mwa Yehova, ndi aumphawi a mwa anthu adzakondwerera mwa Woyera wa Israele. Pakuti woopsa wagoma, ndi wonyoza watha, ndi onse odikira zolakwa alikhidwa; amene apalamulitsa munthu mlandu, namtchera msampha iye amene adzudzula pachipata, nambweza wolungama ndi chinthu chachabe. Chifukwa chake Yehova amene anaombola Abrahamu, atero za banja la Yakobo: Yakobo sadzakhala ndi manyazi tsopano, ngakhale nkhope yake tsopano sidzagwa. Koma pamene iye aona ana ake, ntchito ya manja anga, pakati pa iye, iwo adzayeretsa dzina langa; inde, iwo adzayeretsa Woyera wa Yakobo, nadzaopa Mulungu wa Israele. Iwonso osochera mumzimu adzadziwa luntha, ndi iwo amene ang'ung'udza adzaphunzitsidwa. Tsoka kwa ana opanduka, ati Yehova, amene atenga uphungu koma si pa Ine; napangana pangano opanda mzimu wanga, kuti aonjezere tchimo ndi tchimo; amene ayenda kutsikira ku Ejipito, osafunsa kukamwa kwanga, kudzilimbitsa iwo okha ndi mphamvu za Farao, ndi kukhulupirira mthunzi wa Ejipito! Chifukwa chake mphamvu za Farao zidzakhala kwa inu manyazi, ndi kukhulupirira mthunzi wa Ejipito kudzakhala chisokonezo chanu. Pakuti akalonga ake ali pa Zowani, ndi mithenga yake yafika ku Hanesi. Iwo onse adzakhala ndi manyazi, ndi anthu amene sangapindule nao kanthu, amene sakhala kwa iwo thangata, pena phindu, koma manyazi ndi chitonzo. Katundu wa zilombo za kumwera. M'dziko lovuta ndi lopweteka, kumeneko kuchokera mkango waukazi, ndi wamphongo, mphiri, ndi njoka youluka yamoto, iwo anyamula chuma chao pamsana pa abulu, ndi ang'ono zolemera zao pa malinundu a ngamira, kunka kwa anthu amene sadzapindula nao. Pakuti thangata la Ejipito lili lachabe, lopanda pake; chifukwa chake ndamutcha Wonyada, wokhala chabe. Tsopano pita, ukalembe mauwa pamaso pao pathabwa, nuwalembe m'buku, kuti akakhalebe kunthawi yam'tsogolo, mboni ya masiku onse. Pakuti ali anthu opanduka, ana onama, ana osafuna kumva chilamulo cha Yehova; amene amati kwa alauli, Mtima wanu usapenye; ndi kwa aneneri, Musanenere kwa ife zinthu zoona, munene kwa ife zinthu zamyadi, munenere zonyenga; chokani inu munjira, patukani m'bande, tiletsereni Woyera wa Israele pamaso pathu. Chifukwa chake atero Woyera wa Israele, Popeza inu mwanyoza mau awa, nimukhulupirira nsautso ndi mphulupulu, ndi kukhala m'menemo; chifukwa chake kuipa kumeneku kudzakhala kwa inu monga pogumuka pofuna kugwa, monga potukuka m'khoma lalitali, kugumuka kwake kufika modzidzimutsa dzidzidzi. Ndipo Iye adzagumulapo, monga mbiya ya woumba isweka, ndi kuiswaiswa osaileka; ndipo sipadzapezedwa m'zigamphu zake phale lopalira moto pachoso, ngakhale lotungira madzi padziwe. Pakuti atero Ambuye, Yehova Woyera wa Israele, M'kubwera ndi m'kupuma inu mudzapulumutsidwa; m'kukhala chete ndi m'kukhulupirira mudzakhala mphamvu yanu; ndipo simunafuna. Koma munati, Iai, pakuti tidzathawa pa akavalo; chifukwa chake inu mudzathawadi; ndipo ife tidzakwera pa akavalo aliwiro; chifukwa chake iwo amene akuthamangitsani, adzakhala aliwiro. Chikwi chimodzi chidzathawa pakuwadzudzula mmodzi; pakukudzudzulani anthu asanu mudzathawa; kufikira inu mudzasiyidwa ngati mlongoti pamwamba pa phiri, ndi ngati mbendera pamwamba pa chitunda. Chifukwa chake Yehova adzadikira, kuti akukomereni mtima, ndipo chifukwa chake Iye adzakuzidwa, kuti akuchitireni inu chifundo; pakuti Yehova ndiye Mulungu wa chiweruziro; odala ali onse amene amdikira Iye. Pakuti anthu adzakhala m'Ziyoni pa Yerusalemu; iwe sudzaliranso, Iye ndithu adzakukomera mtima pakumveka kufuula kwako; pakumva Iye adzayankha. Ndipo ngakhale Ambuye adzakupatsani inu chakudya cha nsautso, ndi madzi a chipsinjo, koma aphunzitsi ako sadzabisikanso, koma maso ako adzaona aphunzitsi ako; ndipo makutu ako adzamva mau kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m'menemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere. Ndipo mudzaipitsa chokuta cha mafano ako, osema asiliva, ndi chomata cha mafano ako osungunula agolide; udzawataya ngati kanthu konyansa, udzati kwa iwo, Chokani. Ndipo Mulungu adzapatsa mvula ya mbeu yako, ukaibzale m'nthaka; ndi mkate ndiwo phindu la nthaka, ndipo tirigu wake adzacha bwino ndi kuchuluka; tsiku limenelo ng'ombe zako zidzadya m'madambo akulu. Momwemonso ng'ombe ndi ana a bulu olima nthaka adzadya chakudya chochezera, chimene chapetedwa ndi chokokolera ndi mkupizo. Ndipo pamwamba pa mapiri akulu onse, ndi pa zitunda zonse zazitalitali padzakhala mitsinje ndi micherenje ya madzi, tsiku lophana lalikulu, pamene nsanja zidzagwa. Komanso kuwala kwake kwa mwezi kudzakhala ngati kuwala kwa dzuwa, ndi kuwala kwa dzuwa kudzakula monga madzuwa asanu ndi awiri, monga kuwala kwa masiku asanu ndi awiri, tsiku limenelo Yehova adzamanga bala la anthu ake, nadzapoletsa khana limene anawakantha ena. Taonani, dzina la Yehova lichokera kutali, mkwiyo wake uyaka, malawi ake ndi akulu; milomo yake ili yodzala ndi ukali, ndi lilime lake lili ngati moto wonyambita; ndi mpweya wake uli ngati mtsinje wosefukira, umene ufikira m'khosi, kupeta mitundu ya anthu ndi chopetera cha chionongeko; ndi chapakamwa chalakwitsa, chidzakhala m'nsagwada za anthu. Inu mudzakhala ndi nyimbo, monga usiku, podya phwando lopatulika; ndi mtima wokondwa, monga pomuka wina ndi chitoliro, kufikira kuphiri la Yehova, kuthanthwe la Israele. Ndipo Yehova adzamveketsa mau ake a ulemerero, ndipo adzaonetsa kumenya kwa dzanja lake, ndi mkwiyo wake waukali, ndi lawi la moto wonyambita, ndi kuomba kwa mphepo, ndi mkuntho ndi matalala. Pakuti ndi mau a Yehova Asiriya adzathyokathyoka, ndi ndodo yake adzammenya. Ndipo nthawi zonse Yehova adzawakantha ndi ndodo yosankhikayo, padzamveka mangaka ndi zeze; ndi m'nkhondo zothunyanathunyana, Iye adzamenyana nao. Pakuti Tofeti wakonzedwa kale, inde chifukwa cha mfumu wakonzedweratu; Iye wazamitsapo, nakuzapo; mulu wakewo ndi moto ndi nkhuni zambiri; mpweya wa Yehova uuyatsa ngati mtsinje wa sulufure. Tsoka kwa iwo amene atsikira kunka ku Ejipito kukathandizidwa, natama akavalo; nakhulupirira magaleta, pakuti ali ambiri, ndi okwera pa akavalo, pakuti ali a mphamvu zambiri; koma sayang'ana Woyera wa Israele, ngakhale kumfuna Yehova! Koma Iyenso ndi wanzeru, nadzatengera choipa, ndipo sadzabwezanso mau ake, koma adzaukira banja la ochita zoipa, ndi amene athandiza iwo akugwira ntchito yoipa. Koma Aejipito ndiwo anthu, si Mulungu; ndi akavalo ao ali nyama, si mzimu; ndipo pamene Yehova adzatambasula dzanja lake, wothandiza adzaphunthwa, ndi wothandizidwa adzagwa, ndipo iwo onse awiri pamodzi adzalephera. Pakuti Yehova atero kwa ine, Monga mkango, ndi mwana wa mkango wobangula pa nyama yake, sudzaopa mau a khamu la abusa oitanidwa kuupirikitsa, ngakhale kudzichepetsa wokha, chifukwa cha phokoso lao; motero Yehova wa makamu adzatsikira kumenyana nkhondo kuphiri la Ziyoni, ndi kuchitunda kwake komwe. Monga mbalame ziuluka, motero Yehova wa makamu adzatchinjiriza Yerusalemu; Iye adzatchinjirikiza ndi kuupulumutsa, adzapitirapo ndi kuusunga. Bwerani kwa Iye amene mwampandukira kolimba, ana a Israele inu. Pakuti tsiku limenelo iwo adzataya munthu yense mafano ake asiliva, ndi mafano ake agolide amene manja anuanu anawapanga akuchimwitseni inu. Pamenepo Asiriya adzagwa ndi lupanga losati la munthu; ndi lupanga losati la anthu lidzammaliza iye; ndipo iye adzathawa lupanga, ndi anyamata ake adzalamba. Ndipo mwala wake udzachoka, chifukwa cha mantha, ndi akalonga ake adzaopa mbendera, ati Yehova, amene moto wake uli m'Ziyoni, ndi ng'anjo yake m'Yerusalemu. Taonani mfumu idzalamulira m'chilungamo, ndi akalonga adzalamulira m'chiweruzo. Ndipo munthu adzakhala monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m'malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m'dziko lotopetsa. Ndipo maso a iwo amene aona sadzatsinzina, ndi makutu a iwo amene amva adzamvera. Mtimanso wansontho udzadziwa nzeru, ndi lilime la achibwibwi lidzalankhula zomveka msanga. Wopusa sadzayesedwanso woolowa manja, ngakhale wouma manja sadzayesedwa mfulu. Pakuti wopusa adzanena zopusa, ndi mtima wake udzachita mphulupulu, kuchita zoipitsa, ndi kunena za Yehova molakwira, kusowetsa konse mtima wanjala, ndi kulepheretsa chakumwa cha waludzu. Zipangizonso za womana zili zoipa; iye apangira ziwembu zakuononga waumphawi ndi mau onama, ngakhale pamene wosowa alankhula zoona. Koma mfulu aganizira zaufulu, nakhazikika m'zaufulu zomwe. Ukani, akazi inu, amene mulinkukhala phee, mumve mau anga; inu ana akazi osasamalira, tcherani makutu pa kulankhula kwanga. Pakutha chaka, kudza masiku ena inu mudzavutidwa, inu akazi osasamalira; pakuti masika a mphesa adzasoweka, sadzatuta konse. Nthunthumirani, inu akazi, amene mulinkukhalaphe; vutidwani, inu osasamalira, vulani mukhale maliseche, nimumange chiguduli m'chuuno mwanu. Iwo adzadzimenya pazifuwa chifukwa cha minda yabwino, chifukwa cha mpesa wobalitsa. Pa dziko la anthu anga padzafika minga ndi lunguzi; inde pa nyumba zonse zokondwa, m'mudzi wokondwerera; pakuti nyumba ya mfumu idzasiyidwa; mudzi wa anthu ambiri udzakhala bwinja; chitunda ndi nsanja zidzakhala nkhwimba kunthawi zonse, pokondwera mbidzi podyera zoweta; kufikira mzimu udzathiridwa pa ife kuchokera kumwamba, ndi chipululu chidzasanduka munda wobalitsa, ndi munda wobalitsa udzayesedwa nkhalango. Pamenepo chiweruzo chidzakhala m'chipululu, ndi chilungamo chidzakhala m'munda wobalitsa. Ndi ntchito ya chilungamo idzakhala mtendere; ndi zotsata chilungamo zidzakhala mtendere, ndi kukhulupirika kunthawi zonse. Ndipo anthu anga adzakhala m'malo a mtendere, ndi mokhala mokhulupirika ndi mopuma mwa phee. Koma kudzagwa matalala m'kugwa kwake kwa nkhalango; ndipo mudzi udzagwetsedwa ndithu. Odala muli inu, amene mubzala m'mbali mwa madzi monse, amene muyendetsa mapazi a ng'ombe ndi bulu. Tsoka kwa iwe amene usakaza, chinkana sunasakazidwa; nupangira chiwembu, chinkana sanakupangire iwe chiwembu! Utatha kusakaza, iwe udzasakazidwa; ndipo utatha kupangira chiwembu, iwo adzakupangira iwe chiwembu. Inu Yehova, mutikomere ife mtima; ife talindira Inu; mukhale dzanja lathu m'mawa ndi m'mawa, chipulumutso chathunso m'nthawi ya mavuto. Pa mau a phokoso mitundu ya anthu yathawa; ponyamuka iwe amitundu abalalika. Ndipo zofunkha zanu zidzasonkhanitsidwa, monga ziwala zisonkhana; monga dzombe atumpha, iwo adzatumpha pa izo. Yehova wakwezedwa; pakuti akhala kumwamba; Iye wadzaza Ziyoni ndi chiweruzo ndi chilungamo. Ndipo kudzakhala chilimbiko m'nthawi zako, chipulumutso chambiri, nzeru ndi kudziwa; kuopa kwa Yehova ndiko chuma chake. Taonani, olimba mtima ao angofuula kunja, mithenga ya mtendere ilira kowawa. Njira zamakwalala zikufa, kulibe woyendamo; Asiriya wathyola chipangano, wanyoza midzi, sasamalira anthu. Dziko lirira maliro ndi kulefuka; Lebanoni ali ndi manyazi, nafota; Saroni afanana ndi chipululu; pa Basani ndi Karimele papukutika. Tsopano ndidzauka, ati Yehova; tsopano ndidzanyamuka, tsopano ndidzakwezedwa. Inu mudzatenga pakati ndi mungu, mudzabala ziputu; mpweya wanu ndi moto umene udzakumalizani inu. Ndipo mitundu ya anthu idzanga potentha miyala yanjeresa; monga minga yodulidwa, nitenthedwa ndi moto. Imvani inu amene muli kutali, chimene ndachita ndi inu; amene muli pafupi, vomerezani mphamvu zanga. Ochimwa a m'Ziyoni ali ndi mantha, kunthunthumira kwadzidzimutsa anthu opanda Mulungu. Ndani mwa ife adzakhala ndi moto wakunyeketsa? Ndani mwa ife adzakhala ndi zotentha zachikhalire? Iye amene ayenda molungama, nanena molunjika; iye amene anyoza phindu lonyenga, nasansa manja ake kusalandira zokometsera milandu, amene atseka makutu ake kusamva za mwazi, natsinzina maso ake kusayang'ana choipa; iye adzakhala pamsanje; malo ake ochinjikiza adzakhala malinga amiyala; chakudya chake chidzapatsidwa kwa iye; madzi ake adzakhala chikhalire. Maso ako adzaona mfumu m'kukongola kwake; iwo adzaona dziko lakutali. Mtima wako udzaganizira zoopsa; mlembi ali kuti? Ali kuti iye amene anayesa msonkho? Ali kuti iye amene anawerenga nsanja? Iwe sudzaona anthu aukali, anthu a mau anthulu, amene iwe sungazindikire; a lilime lachibwibwi, limene iwe sungalimve. Tayang'ana pa Ziyoni, mudzi wa zikondwerero zathu; maso ako adzaona, Yerusalemu malo a phee, chihema chimene sichidzasunthidwa, zichiri zake sizidzazulidwa konse, zingwe zake sizidzadulidwa. Koma pamenepo Yehova adzakhala ndi ife m'ulemerero, malo a nyanja zachitando ndi mitsinje; m'menemo ngalawa sizidzayenda ndi ngombo, ngakhale zombo zazikulu sizidzapita pamenepo. Pakuti Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu; Iye adzatipulumutsa. Zingwe zako za ngalawa zamasulidwa; sizinathe kulimbitsa patsinde pa mlongoti wake, sizinathe kufutukula matanga; pamenepo ndipo cholanda chachikulu, chofunkha chinagawanidwa; wopunduka nafumfula. Ndipo wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala; anthu okhala m'menemo, adzakhululukidwa mphulupulu zao. Idzani pafupi, amitundu inu, kuti mumve; mverani anthu inu, dziko ndi zinthu zonse zotulukamo. Pakuti Yehova akwiyira amitundu onse, nachitira ukali khamu lao lonse; Iye wawaononga psiti, wawapereka kukaphedwa. Ophedwa aonso adzatayidwa kunja, ndipo kununkha kwa mitembo yao kudzamveka, ndipo mapiri adzasungunuka ndi mwazi wao. Ndipo makamu onse a kumwamba adzasungunuka, ndi miyamba idzapindika pamodzi ngati mpukutu; makamu ao onse adzafota monga tsamba limafota pampesa ndi kugwa, ndi monga tsamba lifota pamkuyu. Pakuti lupanga langa lakhuta kumwamba; taonani, lidzatsikira pa Edomu, ndi pa anthu amene ndawatemberera, kuti aweruzidwe. Lupanga la Yehova lakhuta ndi mwazi, lanona ndi mafuta ndi mwazi wa anaankhosa, ndi mbuzi, ndi mafuta a impso ya nkhosa zamphongo; pakuti Yehova ali ndi nsembe m'Bozira, ndi ophedwa ambiri m'dziko la Edomu. Ndipo njati zidzatsika ndi iwo, ndi ng'ombe zofula ndi zamphongo; ndi dziko laolao lidzanona ndi mafuta. Pakuti lili tsiku la kubwezera la Yehova, chaka chakubwezera chilango, mlandu wa Ziyoni. Ndipo mitsinjeyo idzasanduka matope akuda, ndi fumbilo lidzasanduka sulufure, ndi dziko lakelo lidzasanduka matope oyaka moto. Sadzazimikai usiku, ngakhale usana; utsi wake udzakwera nthawi zonse; m'mibadwomibadwo lidzakhala labwinja, palibe amene adzapitapo nthawi za nthawi. Koma vuwo ndi nungu zidzakhalamo, ndipo kadzidzi ndi khungubwi adzakhala m'menemo, ndipo Mulungu adzatambalika pamenepo chingwe choongolera cha chisokonezo, ndi chingwe cholungamitsa chilili chosatha kuchita kanthu. Iwo adzaitana mfulu zake zilowe m'ufumu, koma sizidzaonekako; ndi akalonga ake onse adzakhala chabe. Ndipo minga idzamera m'nyumba zake zazikulu, khwisa ndi mitungwi m'malinga mwake; ndipo adzakhala malo a ankhandwe, ndi bwalo la nthiwatiwa. Ndipo zilombo za m'chipululu zidzakomana ndi mimbulu, tonde adzaitana mnzake; inde manchichi adzatera kumeneko, nadzapeza popumira. Kumeneko kadzidzi adzapanga chisa chake, naikira, naumatira, naswa mumthunzi mwake; inde kumeneko miimba idzasonkhana wonse ndi unzake. Funani inu m'buku la Yehova, nimuwerenge; palibe umodzi wa iye udzasowa, palibe umodzi udzasowa unzake; pakuti pakamwa pa Yehova panena, ndipo mzimu wake wasonkhanitsa iwo. Ndipo Iye wachita maere, chifukwa cha zilombozi, ndipo dzanja lake lazigawira dzikolo ndi chingwe, zidzakhala nalo nthawi zonse ku mibadwomibadwo, zidzakhala m'menemo. Chipululu ndi malo ouma adzakondwa; ndipo dziko loti see lidzasangalala ndi kuphuka ngati duwa. Lidzaphuka mochuluka ndi kusangalala, ngakhale kukondwa ndi kuimba; lidzapatsidwa ulemerero wa Lebanoni, ndi ukulu wa Karimele ndi Saroni; anthuwo adzaona ulemerero wa Yehova, ukulu wake wa Mulungu wathu. Limbitsani manja opanda mphamvu, ndi kulimbitsa maondo a gwedegwede. Nenani kwa a mitima ya chinthenthe, Limbani, musaope; taonani, Mulungu wanu adza ndi kubwezera chilango, ndi mphotho ya Mulungu; Iye adzafika ndi kukupulumutsani. Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzaimba; pakuti m'chipululu madzi adzatuluka, ndi mitsinje m'dziko loti see. Ndipo mchenga wong'azimira udzasanduka thamanda, ndi nthaka yopanda madzi idzasanduka zitsime zamadzi; m'malo a ankhandwe m'mene iwo anagona, mudzakhala udzu ndi mabango ndi milulu. Ndipo kudzakhala khwalala kumeneko, ndi njira, ndipo idzatchedwa njira yopatulika; odetsedwa sadzapita m'menemo; koma Iye adzakhala nao oyenda m'njira, ngakhale opusa, sadzasochera m'menemo. Sikudzakhala mkango kumeneko, ngakhale chilombo cholusa sichidzapondapo, pena kupezedwa pamenepo; koma akuomboledwa adzayenda m'menemo; ndipo oomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika ku Ziyoni alikuimba; kukondwa kosatha kudzakhala pa mitu yao; iwo adzakhala ndi kusekerera ndi kukondwa, ndipo chisoni ndi kuusa moyo kudzachoka. Koma panali chaka chakhumi ndi chinai cha mfumu Hezekiya, Senakeribu, mfumu ya Asiriya anadza, nathira nkhondo pa midzi ya malinga yonse ya Yuda, nailanda. Ndipo mfumu ya Asiriya inatumiza kazembe kuchokera pa Lakisi, kunka ku Yerusalemu, kwa mfumu Hezekiya, ndi nkhondo yambiri. Ndipo iye anaima chifupi ndi mcherenje wa thamanda la kumtunda, m'khwalala la pa mwaniko wa wotsuka nsalu. Ndipo anamtulukira Eliyakimu, mwana wa Hilikiya, amene anali wapanyumba, ndi Sebina, mlembi, ndi Yowa, mwana wa Asafu, mkumbutsi. Ndipo kazembeyo anati kwa iwo, Nenani inu tsopano kwa Hezekiya, Itero mfumu yaikulu, mfumu ya Asiriya, Kodi chikhulupiriro ichi nchotani, uchikhulupirira iwe? Ine nditi, Uphungu wako, ndi mphamvu zako za kunkhondo, zingokhala mau achabe; tsopano ukhulupirira yani, kuti wandipandukira ine? Taona, ukhulupirira ndodo yabango iyi yophwanyika, kunena Ejipito; imene munthu akaitsamira, idzalowa m'dzanja mwake, ndi kulipyoza; momwemo Farao, mfumu ya Aejipito, kwa onse amene amkhulupirira iye. Koma ukanena kwa ine, Ife tikhulupirira Yehova Mulungu wathu; kodi si ndiye amene Hezekiya wachotsa misanje yake ndi maguwa ake a nsembe, nati kwa Yuda, ndi kwa Yerusalemu, Inu mudzapembedzera patsogolo pa guwa la nsembe ili? Chifukwa chake upereketu zikole kwa mbuyanga, mfumu ya Asiriya, ndipo ine ndidzakupatsa iwe akavalo zikwi ziwiri, ngati iwe udzaona okwerapo. Bwanji tsono iwe ungathe kubweza nkhope ya nduna mmodzi wamng'ono wa atumiki a mbuyanga, ndi kukhulupirira Ejipito, kuti adzakupatsa magaleta ndi apakavalo? Ndipo ine tsopano, kodi ndafika opanda Yehova kudzamenyana ndi dziko ili, kudzalipasula? Yehova anati kwa ine, Kwera, ndi kumenyana ndi dziko ili, ndi kulipasula. Ndipo Eliyakimu, ndi Sebina, ndi Yowa, anati kwa kazembeyo, Nenanitu kwa atumiki anu m'chinenero cha Aramu; pakuti ife tichimva; ndipo musanene kwa ife m'Chiyuda, m'makutu a anthu amene ali palinga. Koma kazembeyo anati, Kodi mbuyanga ananditumiza ine kwa mbuyako ndi kwa iwe kunena mau amenewa? Kodi iye sananditumize adye ndowe zaozao, ndi kumwa madzi aoao ndi inu? Pamenepo kazembeyo anaima, nafuula ndi mau akulu m'Chiyuda, nati, Imvani, inu, mau a mfumu yaikulu, mfumu ya Asiriya. Mfumu itere, Musaleke Hezekiya anyenge inu; pakuti iye sadzathai kukupulumutsani: ngakhale musaleke Hezekiya akhulupiritse inu kwa Yehova, ndi kunena, Yehova adzatipulumutsa ndithu; mudzi uwu sudzaperekedwa m'manja mwa mfumu ya Asiriya. Musamvere Hezekiya, pakuti mfumu ya ku Asiriya itere, Mupangane nane, tulukirani kwa ine; ndipo yense adye mphesa zake, ndi nkhuyu zake, namwe yense madzi a pa chitsime chake; Kufikira ine ndidzadza, ndi kunka nanu kudziko lofanana ndi lanu, dziko la tirigu ndi vinyo, dziko la chakudya ndi minda yamphesa. Chenjerani angakukopeni inu Hezekiya, ndi kuti, Yehova adzatipulumutsa ife. Kodi milungu iliyonse ya amitundu inapulumutsa dziko lao m'manja mwa mfumu ya ku Asiriya? Ili kuti milungu ya Hamati, ndi Aripadi? Ili kuti milungu ya Sefaravaimu? Kodi inapulumutsa Samariya m'manja mwanga? Mwa milungu yonse ya maiko awa, inapulumutsa dziko lao m'manja mwanga ndi iti, kuti Yehova adzapulumutsa Yerusalemu m'manja mwanga? Koma iwo anakhala chete, osamuyankha mau, pakuti mfumu inawalamulira kuti, Musamuyankhe. Ndipo anafika Eliyakimu, mwana wa Hilikiya, amene anali wapanyumba, ndi Sebina, mlembi, ndi Yowa, mwana wa Asafu, mkumbutsi, kwa Hezekiya ndi zovala zao zong'ambika, namuuza iye mau a kazembeyo. Ndipo panali pamene mfumu Hezekiya anamva, anang'amba zovala zake, navala chiguduli, nalowa m'nyumba ya Yehova. Ndipo anatumiza Eliyakimu, wapanyumba, ndi Sebina, mlembi, ndi akulu a nsembe, atafunda chiguduli, kwa Yesaya, mneneri, mwana wa Amozi. Ndipo iwo anati kwa iye, Hezekiya atere, Tsiku lalero ndilo tsiku la vuto, ndi lakudzudzula ndi chitonzo; pakuti nthawi yake yakubala ana yafika, ndipo palibe mphamvu yobalira. Kapena Yehova Mulungu wako adzamva mau a kazembeyo, amene mfumu ya Asiriya mbuyake inamtuma kukatonza Mulungu wamoyo, nadzadzudzula mau amene Yehova Mulungu wako adawamva; chifukwa chake, kweza pemphero lako chifukwa cha otsala osiyidwa. Ndipo atumiki a mfumu Hezekiya anadza kwa Yesaya. Ndipo Yesaya anati kwa iwo, Mukati kwa mbuyanu, Atero Yehova, musaope mau amene wawamva iwe, amene atumiki a mfumu ya Asiriya andilalatira Ine. Taonani, ndidzaika mzimu mwa iye, ndipo iye adzamva mbiri, nadzabwerera kunka kudziko la kwao; ndipo ndidzamgwetsa ndi lupanga m'dziko la kwao. Ndipo kazembeyo anabwerera, napeza mfumu ya Asiriya ilikuponyana nkhondo ndi Libina; pakuti anamva kuti inachoka ku Lakisi. Ndipo anamva anthu alinkunena za Tirihaka, mfumu ya Kusi, Iye watuluka kudzamenyana ndi iwe. Ndipo pamene anamva, iye anatumiza mithenga kwa Hezekiya ndi kuti, Mukati kwa Hezekiya, mfumu ya Yuda, Asakunyenge Mulungu wako, amene iwe umkhulupirira, ndi kuti, Yerusalemu sadzaperekedwa m'manja mwa mfumu ya Asiriya. Taona, iwe wamva chimene mafumu a Asiriya anachitira maiko onse, ndi kuwapasula konse; ndipo kodi iwe udzapulumutsidwa? Kodi milungu ya amitundu yaipulumutsa iyo, imene atate anga anaipasula? Gozani ndi Harani ndi Rezefe ndi ana a Edeni amene anali m'Telasara. Ili kuti mfumu ya ku Hamati, ndi mfumu ya ku Aripadi, ndi mfumu yamudzi wa ku Sefaravaimu, ya ku Hena, ndi Iva? Ndipo Hezekiya analandira kalatayo m'manja mwa mithengayo, namuwerenga; ndipo Hezekiya anakwera kunka kunyumba ya Yehova, namfunyulula pamaso pa Yehova. Ndipo Hezekiya anapemphera kwa Yehova, nati, Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, amene mukhala pa akerubi, Inu ndinu Mulungu, Inu nokha, wa maufumu onse a dziko lapansi, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi. Tcherani makutu anu, Yehova, nimumve; tsegulani maso anu, Yehova, nimuone; ndi kumva mau onse a Senakeribu, amene watumiza kumtonza Mulungu wamoyo. Zoonadi, Yehova, mafumu a Asiriya anaononga maiko onse, ndi pokhala pao. Ndipo anaponya milungu yao pamoto; pakuti iyo sinali milungu, koma ntchito yopangidwa ndi manja a anthu, mtengo ndi mwala; chifukwa chake iwo anaiononga. Chifukwa chake, Yehova, Mulungu wathu, mutipulumutse ife m'manja mwake, kuti maufumu onse a dziko adziwe, kuti Inu ndinu Yehova, Inu nokha. Ndipo Yesaya, mwana wa Amozi, anatumiza kwa Hezekiya, ndi kuti, Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Popeza wandipemphera za Senakeribu mfumu ya Asiriya, awa ndiwo mau amene Yehova wanena za iye, Namwali, mwana wamkazi wa Ziyoni, wakunyoza iwe ndi kuseka iwe ndi chiphwete; mwana wamkazi wa Yerusalemu wapukusa mutu wake pambuyo pako. Ndani amene, iwe wamtonza ndi kumlalatira? Ndani amene iwe wakwezera mau ako ndi kutukulira maso ako kumwamba? Ndiye Woyera wa Israele. Wamtonza Ambuye ndi atumiki ako, ndipo wati, Ndi khamu la magaleta anga ine ndafika kunsonga za mapiri, kumbali za Lebanoni; ndipo ndidzagwetsapo mikungudza yaitali, ndi milombwa yosankhika; ndipo ine ndidzafika pamutu pake penipeni, kunkhalango ya munda wake wobalitsa. Ine ndakumba ndi kumwa madzi, ndidzaumitsa nyanja zonse za Ejipito ndi kuphazi kwanga. Kodi iwe sunamve, kuti ndinachita ichi kale, ndi kuchikonza nthawi zakale? Tsopano Ine ndachikwaniritsa, kuti iwe ukapasule midzi yamalinga, isanduke miunda. Chifukwa chake okhalamo analefuka, naopsedwa, nathedwa nzeru; ananga udzu wa m'munda, ndi masamba awisi, ndi udzu wa pamachindwi, ndi munda wa tirigu asanakule. Koma ndidziwa pokhala pansi pako, ndi kutuluka kwako, ndi kulowa kwako, ndi kundikwiyira kwako. Chifukwa cha kundikwiyira Ine kwako, ndi popeza kudzikweza kwako kwafika m'makutu mwanga. Ine ndidzaika mbedza yanga m'mphuno mwako, ndi chapakamwa changa m'milomo yako, ndipo ndidzakubweza iwe m'njira yomwe unadzerayo. Ndipo ichi chidzakhala chizindikiro kwa iwe: chaka chino mudzadya zimene zili zomera zokha, ndipo chaka chachiwiri mankhokwe ake; ndipo chaka chachitatu bzalani ndi kudula ndi kulima minda yamphesa ndi kudya chipatso chake. Ndipo otsala amene opulumuka a nyumba ya Yuda adzaphukanso mizu pansi, nadzabala chipatso pamwamba. Pakuti mudzaoneka m'Yerusalemu, otsala ndi opulumuka m'phiri la Ziyoni; changu cha Yehova wa makamu chidzachita ichi. Chifukwa chake atero Yehova za mfumu ya Asiriya, Iye sadzafika pa mudzi uno, ngakhale kuponyapo muvi, ngakhale kufika patsogolo pake ndi chikopa, ngakhale kuunjikirapo mulu. Pa njira yomwe anadzerayo, abwerera yomweyo, ndipo sadzafika pa mudzi uno, ati Yehova. Pakuti ndidzatchinjiriza mudzi uno, kuupulumutsa, chifukwa cha Ine mwini, ndi mtumiki wanga Davide. Ndipo mthenga wa Yehova anatuluka, naphaipha m'zithando za Asiriya, zikwi zana ndi makumi asanu ndi atatu ndi zisanu, ndipo pamene anthu anauka mamawa, taonani, onse ndiwo mitembo. Ndipo Senakeribu, mfumu ya Asiriya, anachoka, namuka, nabwerera, nakhala pa Ninive. Ndipo panali, pamene iye analikupembedzera m'nyumba ya Nisiroki, mulungu wake, Adrameleki ndi Sarezere, ana ake anamupha iye ndi lupanga; ndipo iwo anapulumuka, nathawira ku dziko la ku Ararati. Ndipo Esarahadoni, mwana wake, analamulira m'malo mwake. Masiku amenewo Hezekiya anadwala, nafuna kufa. Ndipo Yesaya mneneri, mwana wa Amozi, anadza kwa iye, nati kwa iye, Atero Yehova, Konza nyumba yako, pakuti iwe udzafa, sudzakhala ndi moyo. Ndipo Hezekiya analoza nkhope yake kukhoma, napemphera kwa Yehova, nati, Kumbukiranitu tsopano, Yehova, kuti ndayenda pamaso panu m'zoonadi ndi mtima wangwiro, ndipo ndachita zabwino pamaso panu. Ndipo Hezekiya analira kolimba. Ndipo anafika mau a Yehova kwa Yesaya, ndi kuti, Ukanene kwa Hezekiya, Atero Yehova, Mulungu wa Davide, kholo lako, Ndamva kupemphera kwako, ndaona misozi yako; taona, ndidzaonjezera pa masiku ako zaka khumi ndi zisanu. Ndipo ndidzakupulumutsa iwe ndi mudzi uno m'manja mwa mfumu ya Asiriya, ndipo ndidzatchinjiriza mudzi uno. Ndipo ichi chidzakhala chizindikiro kwa iwe chochokera kwa Yehova, kuti Yehova adzachita ichi wanenachi; taona, ndidzabweza mthunzi wa pamakwerero, umene watsika pa makwerero a Ahazi ndi dzuwa, ubwerere makwerero khumi. Ndipo dzuwa linabwerera makwerero khumi pamakwerero, pamene udatsika mthunziwo. Malemba a Hezekiya mfumu ya Ayuda muja anadwala, atachira nthenda yake. Ine ndinati, Pakati pa masiku anga ndidzalowa m'zipata za kunsi kwa manda; Ndazimidwa zaka zanga zotsala. Ndinati, Sindidzaona Yehova m'dziko la amoyo; sindidzaonanso munthu pamodzi ndi okhala kunja kuno; Pokhala panga pachotsedwa, pandisunthikira monga hema wa mbusa; Ndapindapinda moyo wanga ngati muomba; Iye adzandidula ine poomberapo; Kuyambira usana kufikira usiku mudzanditsiriza ine. Ndinadzitonthoza kufikira mamawa; monga mkango, momwemo Iye anathyolathyola mafupa anga onse; Kuyambira usana kufikira usiku mudzanditsiriza ine. Ndinalankhulalankhula ngati namzeze, pena chumba; Ndinalira maliro ngati nkhunda; maso anga analephera pogadamira kumwamba. Yehova ndasautsidwa, mundiperekere chikoli. Kodi ndidzanena chiyani? Iye wanena kwa ine, ndiponso Iye mwini wachita ichi; Ine ndidzayenda chete zaka zanga zonse, chifukwa cha zowawa za moyo wanga. Ambuye ndi zinthu izi anthu akhala ndi moyo. Ndipo m'menemo monse muli moyo wa mzimu wanga; Chifukwa chake mundichiritse ine, ndi kundikhalitsa ndi moyo. Taonani, ndinali ndi zowawa zazikulu, chifukwa cha mtendere wanga; Koma Inu mokonda moyo wanga, munaupulumutsa m'dzanja la chivundi, Pakuti mwaponya m'mbuyo mwanu machimo anga onse. Pakuti kunsi kwa manda sikungakuyamikeni Inu; imfa singakulemekezeni; Otsikira kudzenje sangaziyembekeze zoona zanu. Wamoyo, wamoyo, iye adzakuyamikani inu, monga ine lero; Atate adzadziwitsa ana ake zoona zanu. Yehova ndiye wondipulumutsa ine; Chifukwa chake tidzaimba nyimbo zanga, ndi zoimba zazingwe Masiku onse a moyo wathu m'nyumba ya Yehova. Ndipo Yesaya adati, Atenge m'bulu wankhuyu, auike pafundo, ndipo iye adzachira. Hezekiya anatinso, Chizindikiro nchiyani, kuti ndidzakwera kunka kunyumba ya Yehova? Nthawi imeneyo Merodaki-Baladani, mwana wa Baladani, mfumu ya ku Babiloni, anatumiza akalata ndi mphatso kwa Hezekiya; pakuti anamva kuti iye anadwala, nachira. Ndipo Hezekiya anakondwera nao, nawaonetsa nyumba yake ya chuma, siliva, ndi golide, ndi zonunkhira, ndi mafuta okometsera, ndi nyumba yonse ya zida zake, ndi zonse zopezedwa m'zosungira zake; munalibe kanthu m'nyumba mwake, kapena m'dziko lake lonse, kamene Hezekiya sanawaonetse. Ndipo anadza Yesaya mneneri kwa mfumu Hezekiya, nati kwa iye, Kodi anthu awa ananena bwanji, ndipo iwo achokera kuti, kudza kwa inu? Ndipo Hezekiya anati, Iwo achokera ku dziko lakutali, kudza kwa ine, kunena ku Babiloni. Ndipo iye anati, Kodi iwo anaona chiyani m'nyumba mwanu? Ndipo Hezekiya anayankha, Zonse za m'nyumba mwanga iwo anaziona; palibe kanthu ka mwa chuma changa, kamene ine sindinawaonetse. Ndipo Yesaya anati kwa Hezekiya, Imvani mau a Yehova wa makamu. Taona, masiku afika, kuti zonse za m'nyumba mwako, ndi zimene atate wako anazikundika kufikira lero lino, zidzatengedwa kunka ku Babiloni; sipadzatsala kanthu, ati Yehova. Ndipo ana ako amene adzabadwa ndi iwe, amene udzabala, iwo adzawatenga, ndipo adzakhala adindo m'chinyumba chake cha mfumu ya ku Babiloni. Ndipo Hezekiya anati kwa Yesaya, Mau a Yehova, amene iwe wanena, ali abwino. Iye anatinso, Pakuti padzakhala mtendere ndi zoonadi masiku anga. Mutonthoze, mutonthoze mtima wa anthu anga, ati Mulungu wanu. Munene inu zotonthoza mtima kwa Yerusalemu, nimufuulire kwa iye, kuti nkhondo yake yatha, kuti kuipa kwake kwakhululukidwa; kuti iye walandira mowirikiza m'dzanja la Yehova, chifukwa cha machimo ake onse. Mau a wofuula m'chipululu, Konzani njira ya Yehova, lungamitsani m'dziko loti see khwalala la Mulungu wathu. Chigwa chilichonse chidzadzazidwa, ndipo phiri lililonse ndi chitunda chilichonse zidzachepetsedwa, ndipo zokhota zidzaongoledwa, ndipo zamakolokoto zidzasalala; ndipo ulemerero wa Yehova udzavumbulutsidwa, ndipo anthu onse adzauona pamodzi, pakuti pakamwa pa Yehova panena chomwecho. Mau a wina ati, Fuula. Ndipo ndinati, Kodi ndifuule chiyani? Anthu onse ndi udzu, ndi kukoma kwao konse kunga duwa la m'thengo; udzu unyala, duwa lifota; chifukwa mpweya wa Yehova waombapo; zoonadi anthu ndi udzu. Udzu unyala, duwa lifota, koma mau a Mulungu wathu adzakhala nthawi zachikhalire. Iwe amene utengera mau abwino ku Ziyoni, kwera iwe pamwamba pa phiri lalitali; iwe amene utengera mau abwino ku Yerusalemu, kweza mau ako ndi mphamvu, kwezetsa usaope, nena kumidzi ya Yuda, Taonani, Mulungu wanu! Taonani, Ambuye Yehova adzadza ngati wamphamvu, ndipo mkono wake udzalamulira; taonani, mphotho yake ili ndi Iye, ndipo chobwezera chake chili patsogolo pa Iye. Iye adzadyetsa zoweta chake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa anaankhosa pachepa pake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa. Ndani wayesa madzi m'dzanja lake, nayesa thambo ndi chikhato, ndi kudzaza fumbi la nthaka m'nsengwa, ndi kuyesa mapiri m'mbale zoyesera, ndi zitunda m'mulingo? Ndani anapangira mzimu wa Yehova, kapena kukhala phungu lake, ndi kumphunzitsa Iye? Iye anakhala upo ndi yani, ndipo ndani analangiza Iye ndi kumphunzitsa m'njira ya chiweruzo, ndi kumphunzitsa nzeru ndi kumuonetsa njira ya luntha? Taonani, amitundu akunga dontho la m'mtsuko, nawerengedwa ngati fumbi losalala la m'muyeso; taonani atukula zisumbu ngati kanthu kakang'ono. Ndipo Lebanoni sakwanira kutentha, ngakhale nyama zake sizikwanira nsembe yopsereza. Amitundu onse ali chabe pamaso pa Iye; awayesa ngati chinthu chachabe, ndi chopanda pake. Mudzafanizira Mulungu ndi yani tsopano, kapena kumyerekeza ndi chithunzithunzi chotani? Fano losema mmisiri analisungunula, ndipo wosula golide analikuta ndi golide, naliyengera maunyolo asiliva. Wosowa nsembe yoteroyo asankha mtengo umene sungavunde, iye adzisankhira yekha munthu mmisiri waluso, akonze fano losema, limene silisunthika. Kodi inu simunadziwe? Kodi inu simunamve? Kodi sanakuuzeni inu chiyambire? Kodi inu simunadziwitse chiyambire mayambiro a dziko lapansi? Ndi Iye amene akhala pamwamba pa malekezero a dziko lapansi, ndipo okhalamo akunga ziwala; amene afutukula thambo ngati chinsalu, naliyala monga hema wakukhalamo; amene asandutsa akalonga kuti akhale achabe, nasandutsa oweruza a dziko lapansi akhale opanda pake. Inde sanaokedwe, inde sanafesedwe; inde, muzu wao sunazike pansi; koma Iye anawaombetsera mphepo, ndipo afota, ndipo kamvulumvulu awachotsa monga chiputu. Mudzandifanizira Ine ndi yani tsono, kuti ndilingane naye, ati Woyerayo. Kwezani maso anu kumwamba, muone amene analenga izo, amene atulutsa khamu lao ndi kuziwerenga; azitcha zonse maina ao, ndi mphamvu zake zazikulu, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoweka. Bwanji iwe, Yakobo, umati, ndi bwanji umanena iwe, Israele, Njira yanga yabisika kwa Yehova; ndipo chiweruzo cha Mulungu wanga chandipitirira? Kodi iwe sunadziwe? Kodi sunamve? Mulungu wachikhalire, Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi, salefuka konse, salema; nzeru zake sizisanthulika. Iye alimbitsa olefuka, naonjezera mphamvu iye ameme alibe mphamvu. Ngakhale anyamata adzalefuka ndi kulema ndi amisinkhu adzagwa ndithu: koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka. Khalani chete pamaso pa Ine, zisumbu inu, anthu atengenso mphamvu; ayandikire; pamenepo alankhule; tiyeni tiyandikire pamodzi kuchiweruziro. Ndani anautsa wina wochokera kum'mawa, amene amuitana m'chilungamo, afike pa phazi lake? Iye apereka amitundu patsogolo pake, namlamuliritsa mafumu; nawapereka monga fumbi kulupanga lake, monga chiputu chouluzidwa ku uta wake. Iye awathamangitsa, napitirira mwamtendere; pa njira imene asanapitemo ndi mapazi ake. Ndani wachipanga, nachimaliza icho, kutchula mibadwo chiyambire? Ine Yehova, ndine ndemwe. Zisumbu zinaona niziopa; malekezero a dziko lapansi ananthunthumira; anayandikira, nafika. Iwo anathangata yense mnansi wake, ndi yense anati kwa mbale wake, Khala wolimba mtima. Chotero mmisiri wa mitengo analimbikitsa wosula golide, ndi iye amene asalaza ndi nyundo anamlimbikitsa iye amene amenya posulira, nanena za kulumikiza ndi ntovu, Kuli kwabwino; ndipo iye akhomera fanolo misomali kuti lisasunthike. Koma iwe, Israele, mtumiki wanga, Yakobo, amene ndinakusankha, mbeu ya Abrahamu bwenzi langa; iwe amene ndinakuwira iwe zolimba kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, ndi kukuitana iwe kuchokera m'ngodya zake, ndipo ndinati kwa iwe, Ndiwe mtumiki wanga ndakusankha, sindinakutaya kunja; usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo. Taona, onse amene akukwiyira iwe adzakhala ndi manyazi, nasokonezedwa; iwo amene akangana ndi iwe adzakhala ngati chabe, nadzaonongeka. Iwe udzawafuna osawapeza, ngakhale iwo amene akangana ndi iwe; ochita nkhondo ndi iwe, adzakhala ngati chabe, ndi monga kanthu kopanda pake. Pakuti Ine Yehova Mulungu wako ndidzagwira dzanja lako lamanja, ndi kunena kwa iwe, Usaope ndidzakuthandiza iwe. Usaope, Yakobo, nyongolotsi iwe, ndi anthu inu a Israele; ndidzakuthangata iwe, ati Yehova, ndiye Mombolo wako, Woyera wa Israele. Taona, ndidzakuyesa iwe choombera tirigu chatsopano chakuthwa chokhala ndi mano; iwe udzaomba mapiri ndi kuwapera asalale, ndi kusandutsa zitunda mungu. Iwe udzawapeta, ndi mphepo idzawauluza; ndipo kamvulumvulu adzawamwaza; ndipo iwe udzasangalala mwa Yehova, udzadzikuza mwa Woyera wa Israele. Wosauka ndi wosowa afuna madzi, ndipo palibe, ndi lilime lao lilephera, chifukwa cha ludzu; Ine Yehova ndidzawayankha, Ine Mulungu wa Israele sindidzawasiya. Ndidzagwetsa mitsinje pazitunda zoti see, ndi akasupe pakati pa zigwa; ndidzasandutsa chipululu, chikhale thamanda lamadzi, ndi mtunda wouma ukhale magwero a madzi. Ndidzabzala m'chipululu mkungudza, ndi msangu, ndi kasiya, ndi mtengo wa azitona; ndidzaika m'chipululu pamodzi mlombwa, ndi mkuyu, ndi naphini; kuti iwo aone ndi kudziwa, ndi kulingalira, ndi kumvetsa pamodzi, kuti dzanja la Yehova lachita ichi, ndipo Woyera wa Israele wachilenga ichi. Onetsani mlandu wanu, ati Yehova; tulutsani zifukwa zanu zolimba, ati mfumu ya Yakobo. Azitulutse, atitchulire ife, chimene chidzaoneka; tchulani inu zinthu zakale, zinali zotani, kuti ife tiganizire pamenepo, ndi kudziwa mamaliziro ao; kapena tionetseni ife zinthu zimene zilinkudza. Tchulani zinthu zimene zilinkudza m'tsogolo, kuti ife tidziwe kuti inu ndinu milungu; inde, chitani zabwino, kapena chitani zoipa, kuti ife tiopsedwe, ndi kuona pamodzi. Taonani, inu muli achabe, ndi ntchito yanu yachabe; wonyansa ali iye amene asankha inu. Ndautsa wina wakuchokera kumpoto; ndipo iye wafika wakuchokera potuluka dzuwa, amene atchula dzina langa; ndipo iye adzafika pa olamulira, monga matope, ndi monga muumbi aponda dothi la mbiya. Ndani watchula icho chiyambire, kuti ife tichidziwe? Ndi nthawi zakale, kuti ife tinene, Iye ali wolungama? Inde, palibe wina amene atchula, inde, palibe wina amene asonyeza, inde palibe wina amene amvetsa mau anu. Poyamba Ine ndidzati kwa Ziyoni, Taona, taona iwo; ndipo ndidzapereka kwa Yerusalemu wina, amene adza ndi mau abwino. Ndipo pamene ndayang'ana, palibe munthu; ngakhale mwa iwo, palibe phungu, amene angathe kuyankha mau, pamene ndiwafunsa. Taona, iwo onse, ntchito zao zikhala zopanda pake ndi zachabe; mafano ao osungunula ndiwo mphepo ndi masokonezo. Taona Mtumiki wanga, amene ndimgwiriziza; Wosankhika wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; ndaika mzimu wanga pa Iye; Iye adzatulutsira amitundu chiweruziro. Iye sadzafuula, ngakhale kukuwa, pena kumvetsa mau ake m'khwalala. Bango lophwanyika sadzalithyola, ndi lawi lozilala sadzalizima; adzatulutsa chiweruzo m'zoona. Iye sadzalephera kapena kudololoka, kufikira atakhazikitsa chiweruzo m'dziko lapansi; ndipo zisumbu zidzalindira chilamulo chake. Atero Mulungu Yehova, Iye amene analenga thambo, nalifutukula, nayala ponse dziko lapansi, ndi chimene chituluka m'menemo, Iye amene amapatsa anthu a m'menemo mpweya, ndi mzimu kwa iwo amene ayenda m'menemo; Ine Yehova ndakuitana Iwe m'chilungamo, ndipo ndidzagwira dzanja lako ndi kusunga Iwe, ndi kupatsa Iwe ukhale pangano la anthu, ndi kuunika kwa amitundu; kuti utsegule maso akhungu, utulutse am'nsinga m'ndende, ndi iwo amene akhala mumdima, atuluke m'nyumba ya kaidi. Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli; ndipo ulemerero wanga Ine sindidzapereka kwa wina, ngakhale kunditamanda kwa mafano osemedwa. Taona, zinthu zakale zaoneka, ndipo zatsopano Ine ndizitchula; zisanabuke ndidzakumvetsani. Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, ndi matamando ake kuchokera ku malekezero a dziko lapansi; inu amene mutsikira kunyanja, ndi zonse zili m'menemo, zisumbu ndi okhala mommo. Chipululu ndi midzi yake ikweze mau ao, midzi imene Kedara akhalamo; okhala m'Sela aimbe, akuwe kuchokera pamwamba pa mapiri. Apereke ulemerero kwa Yehova, anene matamando ake m'zisumbu. Yehova adzatuluka ngati munthu wamphamvu; adzautsa nsanje ngati munthu wa nkhondo; Iye adzafuula, inde adzakuwa zolimba; adzachita zamphamvu pa adani ake. Ndakhala nthawi yambiri wosalankhula ndakhala chete kudzithungata ndekha; tsopano ndidzafuula ngati mkazi wobala; ndidzapuma modukizadukiza ndi wefuwefu pamodzi. Ndidzapasula mapiri ndi zitunda, ndi kuumitsa zitsamba zao zonse; ndi kusandutsa nyanja zisumbu, ndi kuumitsa matamanda. Ndipo ndidzayendetsa akhungu m'khwalala, limene iwo salidziwa, m'njira zimene iwo sazidziwa ndidzawatsogolera; ndidzawalitsa mdima m'tsogolo mwao, ndi kulungamitsa malo okhota. Zinthu izi Ine ndidzachita, ndipo sindidzawasiya. Iwo adzabwezedwa m'mbuyo, adzakhala ndi manyazi ambiri amene akhulupirira mafano osemedwa, nati kwa mafano oyengeka, Inu ndinu milungu yathu. Imvani, agonthi inu; yang'anani, akhungu inu, kuti muone. Ndani ali wakhungu, koma mtumiki wanga? Pena wagonthi, monga mthenga wanga, amene ndimtumiza? Ndani ali wakhungu monga bwenzi langa, ndi wakhungu monga mtumiki wa Yehova? Iwe waona zinthu zambiri, koma susamalira konse; makutu ako ali otseguka, koma sumva konse. Chinakondweretsa Yehova chifukwa cha chilungamo chake kukuza chilamulo, ndi kuchilemekeza. Koma awa ndiwo anthu olandidwa zao ndi kufunkhidwa; iwo onse agwa m'mauna, nabisidwa m'nyumba za akaidi; alandidwa zao, palibe wowapulumutsa; afunkhidwa ndipo palibe woti, Bwezerani. Ndani mwa inu adzatchera khutu lake pamenepo? Amene adzamvera ndi kumva nthawi yakudza? Ndani anapereka Yakobo, kuti afunkhidwe, ndi Israele, kuti awawanyidwe? Kodi si Yehova? Iye amene tamchimwira, ndi amene iwo anakonda kuyenda m'njira zake, ngakhale kumvera chiphunzitso chake. Chifukwa chake anatsanulira pa iye mkwiyo wake waukali, ndi mphamvu za nkhondo; ndipo unamyatsira moto kuzungulira kwake, koma iye sanadziwe; ndipo unamtentha, koma iye sanachisunge m'mtima. Koma tsopano atero Yehova, amene anakulenga iwe Yakobo, ndi Iye amene anakupanga iwe Israele, Usaope, chifukwa ndakuombola iwe, ndakutchula dzina lako, iwe uli wanga. Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha. Chifukwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wako, Woyera wa Israele, Mpulumutsi wako; ndapatsa Ejipito dombolo lako, Etiopiya ndi Seba m'malo mwako. Pokhala iwe wa mtengo wapatali pamaso panga, ndi wolemekezeka, ndipo ndakukonda iwe; Ine ndidzakuombola ndi anthu, ndi kupereka anthu m'malo mwa moyo wako. Usaope; pakuti Ine ndili ndi iwe; ndidzatenga mbeu zako kuchokera kum'mawa, ndi kusonkhanitsa iwe kuchokera kumadzulo. Ine ndidzati ndi kumpoto, Pereka; ndi kumwera, Usaletse; bwera nao ana anga amuna kuchokera kutali, ndi ana anga akazi kuchokera ku malekezero a dziko lapansi; yense wotchedwa dzina langa, amene ndinamlenga chifukwa cha ulemerero wanga; ndinamuumba iye; inde, ndinampanga iye. Tulutsani anthu akhungu, amene ali ndi maso, ndi agonthi, amene ali ndi makutu. Amitundu onse asonkhane pamodzi, ndi anthu aunjikane; ndani mwa iwo anganene ichi ndi kuonetsa ife zinthu zakale? Atenge mboni zao, kuti avomerezeke ndi olungama; pena amve, nanene zoonadi. Inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndi mtumiki wanga, amene ndakusankha; kuti mundidziwe, ndi kundikhulupirira Ine, ndi kuzindikira, kuti Ine ndine; ndisanakhale Ine, panalibe Mulungu wolengedwa, ngakhale pambuyo panga sipadzakhala wina. Ine, Inetu ndine Yehova; ndipo palibe Mpulumutsi, koma Ine ndekha. Ine ndalalikira, ndipo ndikupulumutsa ndi kumvetsa, ndipo panalibe Mulungu wachilendo pakati pa inu; chifukwa chake inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndipo Ine ndine Mulungu. Inde chiyambire nthawi Ine ndine, ndipo palibe wina wopulumutsa m'dzanja langa; ndidzagwira ntchito, ndipo ndani adzaletsa? Atero Yehova, Mombolo wanu, Woyera wa Israele: Chifukwa cha inu ndatumiza ku Babiloni, ndipo ndidzatsitsira iwo onse monga othawa, ngakhale Ababiloni m'ngalawa za kukondwa kwao. Ine ndine Yehova Woyera wanu, Mlengi wa Israele, Mfumu yanu. Atero Yehova, amene akonza njira panyanja, ndi popita m'madzi amphamvu; amene atulutsa galeta ndi kavalo, nkhondo ndi mphamvu; iwo agona pansi pamodzi sadzaukai; iwo atha, azimidwa ngati lawi. Musakumbukire zidapitazo, ngakhale kulingalira zinthu zakale. Taonani, Ine ndidzachita chinthu chatsopano; tsopano chidzaoneka; kodi simudzachidziwa? Ndidzakonzadi njira m'chipululu, ndi mitsinje m'zidalala. Nyama za m'thengo zidzandilimekeza, ankhandwe ndi nthiwatiwa; chifukwa ndipatsa madzi m'chipululu, ndi mitsinje m'mkhwangwala, ndimwetse anthu anga osankhika; anthu amene ndinadzilengera ndekha, kuti aonetse matamando anga. Komabe iwe sunandiitane Ine, Yakobo; koma iwe walema ndi Ine, Israele. Iwe sunanditengere Ine zoweta zazing'ono za nsembe zopsereza zako; kapena kundilemekeza ndi nsembe zako. Sindinakutumikiritsa ndi nsembe zaufa, kapena kukutopetsa ndi lubani. Iwe sunandigulire Ine nzimbe ndi ndalama, pena kundikhutitsa ndi mafuta a nsembe zako. Koma iwe wanditumikiritsa ndi machimo ako, wanditopetsa ndi mphulupulu zako. Ine, Inedi, ndine amene ndifafaniza zolakwa zako, chifukwa cha Ine mwini; ndipo Ine sindidzakumbukira machimo ako. Undikumbutse Ine; tiyeni, tinenane pamodzi; fotokoza mlandu wako, kuti ukalungamitsidwe. Atate wako woyamba anachimwa, ndi otanthauzira ako andilakwira Ine. Chifukwa chake ndidzaipitsa akulu a Kachisi, ndipo ndidzasanduliza Yakobo akhale temberero, ndi Israele akhale chitonzo. Koma tsopano, imva Yakobo, mtumiki wanga, ndi Israele, amene ndakusankha; atero Yehova, amene anakutenga iwe, nakuumba kuchokera m'mimba, amene adzathangata iwe. Usaope Yakobo, mtumiki wanga ndi iwe, Yesuruni, amene ndakusankha iwe. Pakuti ndidzathira madzi pa dziko limene lilibe madzi, ndi mitsinje pa nthaka youma; ndidzathira mzimu wanga pa mbeu yako, ndi mdalitso wanga pa obadwa ako; ndipo iwo adzaphuka pakati pa udzu, ngati msondodzi m'mphepete mwa madzi. Wina adzati, Ine ndili wa Yehova; ndi wina adzadzitcha yekha ndi dzina la Yakobo, ndipo wina adzalemba ndi dzanja lake, Ndine wa Yehova, ndi kudzitcha yekha ndi mfunda wa Israele. Atero Yehova, mfumu ya Israele ndi Mombolo wake, Yehova wa makamu, Ine ndili woyamba ndi womaliza, ndi popanda Ine palibenso Mulungu. Ndipo ndani adzaitana monga Ine, ndi kulalikira ichi ndi kundilongosolera ichi, chikhazikitsire Ine anthu akale? Milunguyo iwadziwitse zomwe zilinkudza, ndi za m'tsogolo. Musaope inu, musakhale ndi mantha; kodi ndinanena kwa iwe zakale, ndi kuzionetsa zimenezo, ndipo inu ndinu mboni zanga. Kodi popanda Ine aliponso Mulungu? Iai, palibe thanthwe; sindidziwa lililonse. Omwe apanga fano losema onsewo asokonezeka; ndipo zokondweretsa zao sadzapindula nazo kanthu; ndipo mboni zao siziona, kapena kudziwa; kuti akhale ndi manyazi. Ndani wapanga mulungu, kapena kusungunula fano losema losapindula kanthu? Taonani anzake onse adzakhala ndi manyazi, ndi amisiri ake ndi anthu; asonkhane onse pamodzi, aimirire; adzaopa, iwo onse adzakhala ndi manyazi. Wachipala achita zake ndi nsompho, nagwira ntchito ndi makala, nafanizira fanolo ndi nyundo, nagwira ntchito yake ndi mkono wake wamphamvu; inde, ali ndi njala, ndipo mphamvu zake zilephera; iye samwa madzi, nalefuka. Mmisiri wa mitengo atambalitsa chingwe; nalilemba ndi cholembera, nalikonza ndi ncherero, nalilemba ndi zolinganizira, nalifanizira monga maonekedwe a munthu, monga munthu wokongola, kuti likhale m'nyumba. Iye adzidulira yekha mikungudza, natenga mtengo wambawa, ndi wathundu, ndi kudzisankhira yekha wina wa mitengo ya nkhalango; naoka mtengo wamlombwa, mvula niukulitsa. Ndipo udzakhala kuti munthu autenthe; iye natengako, nauotha moto; inde auyatsa, naocha mkate; inde, apanga mulungu, naulambira, naupanga fano losema, naligwadira. Iye atenthako mbali ina pamoto; ndi mbali yinayo adya nyama; akazinga zokazinga nakhuta, inde, aotha moto, nati, Ha, ndakongonoka, ndauona moto. Ndipo chotsalacho apanga mulungu, ngakhale fano lake losema; iye aligwadira, nalipembedza, nalipemphera nati, Ndipulumutse ine, chifukwa kuti ndinu mulungu wanga. Iwo sadziwa, kapena kuzindikira, chifukwa pamaso mwao papakidwa thope, kuti sangaone, ndi m'mitima mwako kuti sangadziwitse. Palibe wina wokumbukira, kapena kudziwa, kapena kuzindikira, ndi kuti, Ndatentha mbali ina pamoto, inde ndaochanso mkate pamakala pake, ndakazinga nyama ndi kuidya; kodi ndichipange chotsala chake, chikhale chonyansa? Ndidzagwadira kodi tsinde la mtengo? Iye adya phulusa; mtima wodzinyenga wampambutsa, kuti iye sangapulumutse moyo wake, pena kunena, Kodi simuli kunama m'dzanja langa lamanja? Kumbukirani zinthu izi, Yakobo; ndi Israele, pakuti iwe ndiwe mtumiki wanga; ndakuumba, iwe ndiwe mtumiki wanga, Israele, sindidzakuiwala. Ine ndafafaniza monga mtambo wochindikira zolakwa zako, ndi monga mtambo machimo ako; bwerera kwa Ine, pakuti ndakuombola. Imbani m'mwamba inu, pakuti Yehova wachichita icho; kuwani inu, mbali za pansi pa dziko; imbani mapiri inu; nkhalango iwe, ndi mitengo yonse m'menemo; chifukwa kuti Yehova wapulumutsa Yakobo, ndipo adzadzilemekezetsa yekha mwa Israele. Atero Yehova, Mombolo wako, ndi Iye amene anakuumba iwe m'mimba, Ine ndine Yehova, amene ndipanga zinthu zonse, ndi kufunyulula ndekha zakumwamba, ndi kuyala dziko lapansi; ndani ali ndi Ine? Ndine amene nditsutsa zizindikiro za matukutuku, ndi kuchititsa misala oombeza ula; ndi kubwezera m'mbuyo anthu anzeru, ndi kupusitsa nzeru zao: Ndine amene ndilimbitsa mau a mtumiki wanga, kuchita uphungu wa amithenga anga; ndi kunena za Yerusalemu, Adzakhalamo anthu; ndi za midzi ya Yuda; Idzamangidwa; ndipo ndidzautsa malo abwinja ake. Ndine amene nditi kwa nyanja yakuya, Iphwa, ndipo ndidzaumitsa nyanja zako; ndi kunena za Kirusi, Iye ndiye mbusa wanga, ndipo adzachita zofuna zanga zonse; ndi kunena za Yerusalemu, Adzamangidwa; ndi kwa Kachisi, Maziko ako adzaikidwa. Atero Yehova kwa wodzozedwa wake kwa Kirusi, amene dzanja lake lamanja ndaligwiritsa, kuti agonjetse mitundu ya anthu pamaso pake, ndipo ndidzamasula m'chuuno mwa mafumu; atsegule zitseko pamaso pake, ndi zipata sizidzatsekedwa: Ndidzakutsogolera ndi kusalaza pokakala; ndidzathyolathyola zitseko zamkuwa, ndi kudula pakati akapichi achitsulo; ndipo ndidzakupatsa iwe chuma cha mumdima, ndi zolemera zobisika za m'malo am'tseri, kuti iwe udziwe kuti Ine ndine Yehova, amene ndikuitana iwe dzina lako, ndine Mulungu wa Israele. Ndakuitana iwe dzina lako, chifukwa cha Yakobo mtumiki wanga ndi Israele wosankhidwa wanga; ndakuonjezera dzina, ngakhale iwe sunandidziwa Ine. Ine ndili Yehova, ndipo palibe winanso; popanda Ine palibe Mulungu; ndidzakumanga m'chuuno, ngakhale sunandidziwa; kuti anthu akadziwe kuchokera kumatulukiro a dzuwa ndi kumadzulo, kuti palibe wina popanda Ine; Ine ndine Yehova, palibe winanso. Ine ndilenga kuyera ndi mdima, Ine ndilenga mtendere ndi choipa, Ine ndine Yehova wochita zinthu zonse zimenezi. Igwani pansi, inu m'mwamba, kuchokera kumwamba, thambo litsanulire pansi chilungamo; dziko lapansi litseguke, kuti libalitse chipulumutso, nilimeretse chilungamo chimere pamodzi; Ine Yehova ndinachilenga chimenecho. Tsoka kwa iye amene akangana ndi Mlengi wake! Phale mwa mapale a dziko lapansi! Kodi dongo linganene kwa iye amene aliumba, Kodi upanga chiyani? Pena ntchito yako, Iye alibe manja? Tsoka kwa iye amene ati kwa atate wake, Kodi iwe ubalanji? Pena kwa mkazi, Ulikusauka ninji iwe? Atero Yehova Woyera wa Israele ndi Mlengi wake, Ndifunse Ine za zinthu zimene zilinkudza; za ana anga amuna, ndi za ntchito ya manja anga, ndilamulireni Ine. Ine ndalenga dziko lapansi, ndalengamo munthu; Ine, ngakhale manja anga, ndafunyula kumwamba, ndi zonse za m'menemo, ndinazilamulira ndine. Ine ndautsa Kirusi m'chilungamo, ndipo ndidzalungamitsa njira zake zonse; iye adzamanga mudzi wanga, nadzaleka andende anga anke mwaufulu, wosati ndi mtengo pena mphotho, ati Yehova wa makamu. Atero Yehova, Ntchito ya Ejipito, ndi malonda a Kusi, ndi a Seba, amuna amsinkhu adzakugonjera, nadzakhala ako; nadzakutsata pambuyo m'maunyolo; adzakugonjera, nadzakugwira; adzakupembedza ndi kunena, Zoona Mulungu ali mwa iwe; ndipo palibenso wina, palibe Mulungu. Ndithu Inu ndinu Mulungu, amene mudzibisa nokha, Mulungu wa Israele, Mpulumutsi. Iwo adzakhala ndi manyazi, inde, adzathedwa nzeru onsewo; adzalowa m'masokonezo pamodzi, amene apanga mafano. Koma Israele adzapulumutsidwa ndi Yehova ndi chipulumutso chosatha; inu simudzakhala ndi manyazi, pena kuthedwa nzeru kunthawi zosatha. Pakuti atero Yehova amene analenga kumwamba, Iye ndiye Mulungu amene anaumba dziko lapansi, nalipanga; Iye analikhazikitsa, sanalilenge mwachabe; Iye analiumba akhalemo anthu; Ine ndine Yehova; ndipo palibenso wina. Ine sindinanena m'tseri m'malo a dziko la mdima; Ine sindinati kwa mbeu ya Yakobo, Mundifune Ine mwachabe; Ine Yehova ndinena chilungamo, ndinena zimene zili zoona. Sonkhanani nokha, mudze; yandikirani chifupi pamodzi, inu amene mwapulumuka amitundu; iwo alibe nzeru, amene anyamula mtengo wa fano lao losema, ndi kupemphera mulungu wosakhoza kupulumutsa. Nenani inu, tulutsani mlandu wanu; inde, achite uphungu pamodzi; ndani waonetsa ichi chiyambire nthawi yakale? Ndani wanena ichi kale? Kodi si ndine Yehova? Ndipo palibenso Mulungu wina popanda Ine; Mulungu wolungama, ndi Mpulumutsi; palibenso wina popanda Ine. Yang'anani kwa Ine, mupulumutsidwe, inu malekezero onse a dziko; pakuti Ine ndine Mulungu, palibe wina. Ndadzilumbira ndekha, mau achokera m'kamwa mwanga m'chilungamo, ndipo sadzabwerera, kuti mabondo onse adzandigwadira Ine, malilime onse nadzalumbira Ine. Koma mwa Yehova yekha, wina adzati kwa Ine, muli chilungamo ndi mphamvu; ngakhale kwa Iyeyo anthu adzafika, ndi onse amene anamkwiyira, adzakhala ndi manyazi. Mwa Yehova mbeu yonse ya Israele idzalungamitsidwa ndi kudzikuza. Beli agwada pansi, Nebo awerama; mafano ao ali pa zoweta, ndi pa ng'ombe; zinthu zimene inu munanyamula ponseponse ziyesedwa mtolo, katundu wakulemetsa nyama. Milunguyo iwerama, igwada pansi pamodzi; singapulumutse katundu, koma iyo yeni yalowa m'ndende. Mverani Ine, banja la Yakobo, ndi otsala onse a banja la Israele, amene ndakunyamulani kuyambira m'mimba, ndi kukusenzani chibadwire; ngakhale mpaka mudzakalamba Ine ndine, ndipo ngakhale mpaka tsitsi laimvi, Ine ndidzakusenzani inu; ndalenga, ndipo ndidzanyamula; inde, ndidzasenza, ndipo ndidzapulumutsa. Kodi mudzandifanizira ndi yani, ndi kundilinganiza ndi kundiyerekeza, kuti ife tifanane? Amene ataya golide, namtulutsa m'thumba, ndi kuyesa siliva ndi muyeso, iwo alemba wosula golide; iye napanga nazo mulungu; iwo agwada pansi, inde alambira. Iwo amanyamula mlunguwu paphewa, nausenza, naukhazika m'malo mwake, nukhala chilili; pamalo pakepo sudzasunthika; inde, wina adzaufuulira, koma sungathe kuyankha, kapena kumpulumutsa m'zovuta zake. Kumbukirani ichi, nimuchilimike, mudzikumbutsenso, olakwa inu. Kumbukirani zinthu zoyamba zakale, kuti Ine ndine Mulungu, ndipo palibenso wina; Ine ndine Yehova, ndipo palibenso wina wofana ndi Ine; ndilalikira za chimaliziro kuyambira pachiyambi, ndi kuyambira nthawi zakale ndinena zinthu zimene zisanachitidwe; ndi kunena, Uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzachita zofuna zanga zonse; ndiitana mbalame yolusa kuchokera kum'mawa, ndiye munthu wa uphungu wanga, kuchokera kudziko lakutali; inde, ndanena, ndidzachionetsa; ndinatsimikiza mtima, ndidzachichitanso. Mverani Ine, inu olimba mtima, amene muli kutali ndi chilungamo; ndiyandikizitsa chifupi chilungamo changa sichidzakhala patali, ndipo chipulumutso changa sichidzachedwa; ndipo ndidzaika chipulumutso m'Ziyoni, cha kwa Israele ulemerero wanga. Tsika, ukhale m'fumbi, namwaliwe, mwana wamkazi wa Babiloni; khala pansi popanda mpando wachifumu, mwana wamkazi wa Ababiloni, pakuti iwe sudzayesedwanso wozizira ndi wololopoka. Tenga mipero, nupere ufa; chotsa chophimba chako, vula chofunda, kwinda m'mwendo, oloka mitsinje. Maliseche ako adzakhala osafundidwa, inde, manyazi ako adzaoneka; ndidzachita kubwezera, osasamalira munthu. Mombolo wathu, Yehova wa makamu ndi dzina lake, Woyera wa Israele. Khala iwe chete, lowa mumdima, mwana wamkazi wa Ababiloni; pakuti sudzatchedwanso mkazi wa maufumu. Ndinakwiyira anthu anga, ndinaipitsa cholowa changa, ndi kuwapereka m'manja ako; koma iwe sunawaonetsera chifundo; wasenzetsa okalamba goli lako lolemera ndithu. Ndipo unati, Ndidzakhala mkazi wa mfumu wa nthawi zonse; ndipo sunasamalira izi mumtima mwako, kapena kukumbukira chomalizira chake. Chifukwa chake tsono, imva ichi, iwe wotsata zokondweretsa, amene umakhala mosatekeseka, amene umati mumtima mwako, Ine ndine, ndipo popanda ine palibenso wina; sindidzakhala monga mkazi wamasiye, kapena kudziwa kumwalira kwa ana; koma izi ziwiri zidzakugwera mwadzidzidzi, tsiku limodzi kumwalira kwa ana ndi umasiye zidzakugwera; mokwanira monse, pakati pa maphenda ako ambirimbiri. Pakuti wakhulupirira zoipa zako, wati, Palibe wondiona ine; nzeru zako ndi chidziwitso chako zakusandutsa woipa; ndipo wanena mumtima mwako, Ndine, ndipo popanda ine palibenso wina. Chifukwa chake choipa chidzafika pa iwe; sudzadziwa kucha kwake, ndipo chionongeko chidzakugwera; sudzatha kuchikankhira kumbali; ndipo chipasuko chosachidziwa iwe chidzakugwera mwadzidzidzi. Taima tsopano ndi maphendo ako, ndi unyinji wa matsenga ako, m'menemo iwe unagwira ntchito chiyambire ubwana wako; kuti kapena udzatha kupindula, kuti kapena udzapambana. Watopa mu uphungu wako wambiri; aimirire tsopano openda zam'mwamba, oyang'ana nyenyezi, akuneneratu mwezi ndi mwezi, ndi kukupulumutsa pa zinthu zimene zidzakugwera. Taona, iwo adzakhala ngati ziputu, moto udzawatentha iwo; sadzadzipulumutsa okha kumphamvu za malawi; motowo sudzakhala khala loothako, pena moto wakukhalako. Zinthu zomwe unagwira ntchito yake, zidzatero nawe; iwo amene anachita malonda ndi iwe chiyambire pa ubwana wako, adzayenda yense kunka kumalo kwake; sipadzakhala wopulumutsa iwe. Imvani inu ichi, banja la Yakobo, amene mutchedwa ndi dzina la Israele, amene munatuluka m'madzi a Yuda amene mulumbira dzina la Yehova ndi kutchula dzina la Mulungu wa Israele, koma si m'zoona, pena m'chilungamo. Pakuti adziyesa okha a mudzi wopatulika, ndi kudzikhazikitsa iwo okha pa Mulungu wa Israele; dzina lake ndi Yehova wa makamu. Ndanena zinthu zoyamba kuyambira kale; inde, izo zinatuluka m'kamwa mwanga, ndipo ndinazisonyeza; mwadzidzidzi ndinazichita izo, ndipo zinaoneka. Popeza ndinadziwa, kuti uli wokanika, ndi khosi lako lili mtsempha wachitsulo, ndi mphumi yako mkuwa; chifukwa chake ndinakudziwitsa ichi kuyambira kale; chisanaoneke ndinakusonyeza icho, kuti iwe unganene, Fano langa lachita izo, ndi chifaniziro changa chosema, ndi chifaniziro changa choyenga zinazilamulira. Iwe wachimva; taona zonsezi; ndipo inu kodi inu simudzachinena? Ndakusonyeza iwe zinthu zatsopano kuchokera nthawi yino, ngakhale zinthu zobisika, zimene iwe sunazidziwe. Zalengedwa tsopano, zosati kuyambira kale; ndipo lisanafike tsiku laleroli iwe sunazimve; unganene, Taonani, ndinazidziwa. Inde, iwe sunamva; inde, sunadziwe; inde kuyambira kale khutu lako silinatsegudwe; pakuti ndinadziwa kuti iwe wachita mwachiwembu ndithu, ndipo unayesedwa wolakwa chibadwire. Chifukwa cha dzina langa ndidzachedwetsa mkwiyo wanga, ndi chifukwa cha kutamanda kwanga ndidzakulekerera, kuti ndisakuchotse. Taona ndakuyenga, koma si monga siliva, ndakuyesa iwe m'ng'anjo ya masautso. Chifukwa cha Ine ndekha, chifukwa cha Ine ndekha ndidzachita ichi, pakuti dzina langa lidetsedwerenji? Ndi ulemerero wanga sindidzaupereka kwa wina. Mverani Ine, Yakobo ndi Israele, oitanidwa anga, Ine ndine; ndine woyamba, Inenso ndine womaliza. Inde dzanja langa linakhazika maziko a dziko lapansi, ndi dzanja langa lamanja linafunyulula m'mwamba; pakuziitana Ine ziimirira pamodzi. Sonkhanani inu nonse ndi kumva, ndani mwa iwo aonetsa zinthu izi? Iye amene Yehova anamkonda, iye adzachita kufuna kwake pa Babiloni, ndi mkono wake udzakhala pa Ababiloni. Ine, ngakhale Ine ndanena; inde ndamwitana iye, ndamfikitsa, ndipo adzapindula nayo njira yake. Idzani inu chifupi ndi Ine, imvani ichi; kuyambira pa chiyambi sindinanene m'tseri; chiyambire zimenezi, Ine ndilipo; ndipo tsopano Ambuye Mulungu wanditumiza Ine ndi mzimu wake. Atero Yehova, Mombolo wako, Woyera wa Israele, Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m'njira yoyenera iwe kupitamo. Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja; mbeu yakonso ikadakhala monga mchenga, ndi obadwa a m'chuuno mwako momwemo; dzina lake silikadachotsedwa, pena kuonongeka pamaso panga. Tulukani inu m'Babiloni, athaweni Ababiloni; ndi mau akuimba nenani inu, bukitsani ichi, lalikirani ichi, ngakhale ku malekezero a dziko; nenani, Yehova waombola mtumiki wake Yakobo. Ndipo iwo sanamve ludzu, pamene Iye anawatsogolera m'mapululu; anawatulutsira madzi kutuluka m'matanthwe; anadulanso thanthwe, madzi nabulika. Kulibe mtendere, ati Yehova, kwa oipa. Mverani Ine, zisumbu inu, mumvere anthu inu akutali; Yehova anandiitana Ine ndisanabadwe; m'mimba mwa amai Iye anatchula dzina langa; nachititsa pakamwa panga ngati lupanga lakuthwa, mu mthunzi wa dzanja lake wandibisa Ine; wandipanga Ine; muvi wotuulidwa; m'phodo mwake Iye wandisungitsa Ine, nati kwa Ine, Iwe ndiwe mtumiki wanga, Israele, amene ndidzalemekezedwa nawe. Koma ndinati, Ndagwira ntchito mwachabe, ndatha mphamvu zanga pachabe, ndi mopanda pake; koma ndithu chiweruziro changa chili ndi Yehova, ndi kubwezera kwanga kuli ndi Mulungu wanga. Ndipo tsopano, ati Yehova, amene anandiumba Ine ndisanabadwe ndikhale mtumiki wake, kubwezanso Yakobo kwa Iye, ndi kuti Israele asonkhanidwe kwa Iye; chifukwa Ine ndili wolemekezeka pamaso pa Yehova, ndipo Mulungu wanga wakhala mphamvu zanga; inde, ati, Chili chinthu chopepuka ndithu kuti Iwe ukhale mtumiki wanga wakuutsa mafuko a Yakobo, ndi kubwezera osungika a Israele; ndidzakupatsanso ukhale kuunika kwa amitundu, kuti ukhale chipulumutso changa mpaka ku malekezero a dziko lapansi. Atero Yehova, Mombolo wa Israele, ndi Woyera wake, kwa Iye amene anthu amnyoza, kwa Iye amene mtundu wathu unyasidwa naye, kwa mtumiki wa olamulira: Mafumu adzaona, nadzauka; akalonga nadzalambira chifukwa cha Yehova, amene ali wokhulupirika, ngakhale Woyera wa Israele, amene anakusankha Iwe. Atero Yehova, Nthawi yondikomera ndakuyankha Iwe, ndi tsiku la chipulumutso ndakuthandiza; ndipo ndidzakusunga ndi kupatsa Iwe ukhale pangano la anthu, kuti ukhazikitse dziko, nuwalowetse m'zolowa zopasuka m'malo abwinja; ndi kunena kwa iwo amene ali omangidwa, Mukani, kwa iwo amene ali mumdima, Dzionetseni nokha. Iwo adzadya m'njira, ndi m'zitunda zonse zoti see mudzakhala busa lao. Iwo sadzakhala ndi njala, pena ludzu; ngakhale thukuta, pena dzuwa silidzawatentha; pakuti Iye amene wawachitira chifundo, adzawatsogolera, ngakhale pa akasupe a madzi adzawatsogolera. Ndipo ndidzasandutsa mapiri anga onse akhale njira, ndipo makwalala anga adzakwezeka. Taonani, awa adzachokera kutali; ndipo taonani, awa ochokera kumpoto, ndi kumadzulo; ndi awa ochokera kudziko la Asuwani. Imbani inu, m'mwamba, nukondwere iwe dziko lapansi, imbani inu mapiri, pakuti Yehova watonthoza mtima wa anthu ake, nadzachitira chifundo ovutidwa ake. Koma Ziyoni anati, Yehova wandisiya ine, ndipo Ambuye wandiiwala ine. Kodi mkazi angaiwale mwana wake wa pabere, kuti iye sangachitire chifundo mwana wombala iye? Inde awa angaiwale, koma Ine sindingaiwale iwe. Taona ndakulembera iwe pa zikhato za manja anga; makoma ako alipo masiku onse pamaso panga. Ana ako afulumira; opasula ako ndi iwo amene anakusakaza adzachoka pa iwe. Tukula maso ako kuunguzaunguza, nuone; onsewa asonkhana pamodzi, nadza kwa iwe. Pali Ine, ati Yehova, iwe ndithu udzadziveka wekha ndi iwo onse, monga ndi chokometsera, ndi kudzimangira nao m'chuuno ngati mkwatibwi. Pakuti, kunena za malo ako osiyidwa ndi abwinja ndi dziko lako limene lapasulidwa tsopano, ndithu iwe udzakhala wochepera okhalamo, ndi iwo amene anakumeza iwe adzakhala kutali. Ana ako amasiye adzanena m'makutu ako, Malo andichepera ine, ndipatse malo, kuti ndikhalemo. Pamenepo udzati m'mtima mwako, Ndani wandibalitsa ine amenewa, popeza ana anga anachotsedwa kwa ine, ndipo ndili wouma, ndi wochotsedwa m'dziko, ndi woyendayenda kwina ndi kwina? Ndipo ndani wadza ndi awa? Taona ndinasiyidwa ndekha, amenewa anali kuti? Atero Ambuye Yehova, Taona ndidzakodola anthu a mitundu, ndi kukwezera anthu mbendera yanga; ndipo adzabwera nao ana ako amuna pa chifuwa chao, ndi ana ako akazi adzatengedwa pa mapewa ao. Ndipo mafumu adzakulera, ndi akazi ao akulu adzakuyamwitsa; iwo adzakugwadira ndi nkhope zao zoyang'ana pansi, nadzaseteka fumbi la m'mapazi ako: ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndi iwo amene alindira Ine sadzakhala ndi manyazi. Kodi chofunkha chingalandidwe kwa wamphamvu, pena am'nsinga a woopsa angapulumutsidwe? Koma atero Yehova, Ngakhale am'nsinga a wamphamvu adzalandidwa, ndi chofunkha cha woopsa chidzapulumutsidwa; pakuti Ine ndidzakangana naye amene akangana ndi iwe, ndipo ndidzapulumutsa ana ako. Ndipo ndidzadyetsa iwo amene atsendereza iwe ndi nyama yaoyao; ndi mwazi waowao; iwo adzaledzera monga ndi vinyo wotsekemera; anthu onse adzadziwa kuti Ine Yehova ndili Mpulumutsi wako, ndi Mombolo wako, Wamphamvu wa Yakobo. Atero Yehova, Kalata wa chilekaniro cha amai ako ali kuti amene ndinamsudzula naye? Pena ndani wa angongole anga amene ndamgulitsa iwe? Taona chifukwa cha zoipa zanu munagulitsidwa, ndi chifukwa cha kulakwa kwanu amanu anachotsedwa. Chifukwa chanji ndinafika osapeza munthu? Ndi kuitana koma panalibe wina woyankha? Kodi dzanja langa lafupika konse, kuti silingathe kuombola? Pena Ine kodi ndilibe mphamvu zakupulumutsa? Taona pa kudzudzula kwanga ndiumitsa nyanja, ndi kusandutsa mitsinje chipululu; nsomba zake zinunkha chifukwa mulibe madzi, nizifa ndi ludzu. Ndiveka thambo ndi kuda, ndi kuyesa chiguduli chofunda chake. Ambuye Yehova wandipatsa Ine lilime la ophunzira, kuti ndidziwe kunena mau akuchirikiza iye amene ali wolema. Iye andigalamutsa m'mawa ndi m'mawa, nagalamutsa khutu langa kuti limve monga ophunzira. Ambuye Yehova watsegula khutu langa, ndipo sindinakhala wopanduka ngakhale kubwerera m'mbuyo. Ndinapereka msana wanga kwa omenya, ndi masaya anga kwa iwo amene anakudzula tsitsi langa; sindinabisira nkhope yanga manyazi ndi kulavulidwa. Pakuti Ambuye Yehova adzandithangata Ine; chifukwa chake sindinasokonezedwa; chifukwa chake ndakhazika nkhope yanga ngati mwala, ndipo ndidziwa kuti sindidzakhala ndi manyazi. Iye ali pafupi amene alungamitsa Ine; ndani adzakangana ndi Ine? Tiyeni tiimirire tonse pamodzi; mdani wanga ndani? Andiyandikire. Taonani, Ambuye Yehova adzathandiza Ine; ndani amene adzanditsutsa? Taonani, iwo onse adzatha ngati chovala, njenjete zidzawadya. Ndani ali mwa inu amene amaopa Yehova, amene amamvera mau a mtumiki wake? Iye amene ayenda mumdima, ndipo alibe kuunika, akhulupirire dzina la Yehova, ndi kutsamira Mulungu wake. Taonani, inu nonse amene muyatsa moto, amene mudzimangira m'chuuno ndi nsakali, yendani inu m'chilangali cha moto wanu, ndi pakati pa nsakali zimene mwaziyatsa. Ichi mudzakhala nacho cha pa dzanja langa; mudzagona pansi ndi chisoni. Mverani Ine, inu amene mutsata chilungamo, inu amene mufuna Yehova; yang'anani kuthanthwe, kumene inu munasemedwamo, ndi kuuna kwa dzenje, kumene inu munakumbidwamo. Yang'anani kwa Abrahamu kholo lanu, ndi kwa Sara amene anakubalani inu; pakuti pamene iye anali mmodzi yekha ndinamuitana iye; ndipo ndinamdalitsa ndi kumchulukitsa. Pakuti Yehova watonthoza mtima wa Ziyoni, watonthoza mtima wa malo ake onse abwinja; ndipo wasandutsa chipululu chake ngati Edeni, ndi nkhwangwara yake ngati munda wa Yehova; kukondwa ndi kusangalala kudzapezedwa m'menemo, mayamikiro, ndi mau a nyimbo yokoma. Mverani Ine, inu anthu anga, ndi kunditcherera makutu, iwe, mtundu wa anthu anga; pakuti lamulo lidzachokera kwa Ine, ndipo ndidzakhazikitsa chiweruziro changa chikhale kuunika kwa anthu. Chilungamo changa chili pafupi, chipulumutso changa chamuka; ndipo mikono yanga idzaweruza anthu; zisumbu zidzandilindira, ndipo adzakhulupirira mkono wanga. Tukulani maso anu kumwamba, ndipo muyang'ane pansi pa dziko pakuti kumwamba kudzachoka ngati utsi, ndi dziko lidzatha ngati chofunda, ndipo iwo amene akhala m'menemo adzafa ngati njenjete; koma chipulumutso changa chidzakhala kunthawi zonse, ndi chilungamo changa sichidzachotsedwa. Mverani Ine, inu amene mudziwa chilungamo, anthu amene mumtima mwao muli lamulo langa; musaope chitonzo cha anthu, ngakhale kuopsedwa ndi kutukwana kwao. Pakuti njenjete idzawadya ngati chofunda, ndi mbozi zidzawadya ngati ubweya; koma chilungamo changa chidzakhala kunthawi zonse, ndi chipulumutso changa kumibadwo yonse. Galamuka, galamuka, khala ndi mphamvu, mkono wa Yehova; galamuka monga masiku akale, mibadwo ya nthawi zakale. Kodi si ndiwe amene unadula Rahabu zipinjirizipinjiri; amene unapyoza chinjoka chamnyanja chija? Kodi si ndiwe amene unaumitsa nyanja, madzi akuya kwambiri; anasandutsa nyanja zikhale njira ya kupitapo oomboledwa? Ndipo oomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika ku Ziyoni; ndi nyimbo ndi kukondwa kosatha kudzakhala pa mitu yao; adzakhala m'kusangalala ndi kukondwa, ndipo chisoni ndi kuusa moyo kudzachoka. Ine, Inedi, ndine amene nditonthoza mtima wako; kodi iwe ndani, kuti uopa munthu amene adzafa, ndi mwana wa munthu amene adzakhala ngati udzu; waiwala Yehova Mlengi wako, amene anayala m'mwamba, nakhazika maziko a dziko lapansi, ndi kuopabe tsiku lonse chifukwa cha ukali wa wotsendereza, pamene iye akonzeratu kupasula? Uli kuti ukali wa wotsendereza? Wam'nsinga wowerama adzamasulidwa posachedwa; sadzafa ndi kutsikira kudzenje, chakudya chake sichidzasowa. Pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wako, amene ndiutsa nyanja, kuti mafunde ake akokome; Yehova wa makamu ndi dzina lake. Ndipo ndaika mau anga m'kamwa mwako; ndipo ndakuphimba ndi mthunzi wa dzanja langa, kuti ndikhazike kumwamba ndi kuika maziko a dziko lapansi, ndi kunena kwa Ziyoni, Inu ndinu anthu anga. Galamuka, galamuka, imirira Yerusalemu amene unamwa m'dzanja la Yehova chikho cha ukali wake; iwe wamwa mbale ya chikho chonjenjemeretsa ndi kuchigugudiza. Palibenso wina wakumtsogolera mwa ana amuna onse, amene iye anawabala; palibe wina amgwira dzanja mwa ana onse anawalera. Izi ziwiri zakugwera; ndani adzakulira iwe? Bwinja ndi chipasuko, njala ndi lupanga; ndidzatonthoza mtima wako bwanji? Ana ako amuna akomoka; agona pamtu pa makwalala onse, monga nswala muukonde; adzala ndi ukali wa Yehova, kudzudzula kwa Mulungu wako. Chifukwa chake imva ichi tsopano, iwe wovutidwa ndi woledzera koma si ndi vinyo ai; atero Ambuye ako Yehova, ndi Mulungu wako amene anena mlandu wa anthu ake, Taona, ndachotsa m'dzanja mwako chikho chonjenjemeretsa, ngakhale mbale ya chikho cha ukali wanga; iwe sudzamwa icho kawirinso. Ndidzachiika m'dzanja la iwo amene avutitsa iwe; amene anena kumoyo wako, Gwada pansi kuti ife tipite; ndipo iwe wagonetsa pamsana pako monga pansi, ndi monga khwalala kwa iwo amene apita pamenepo. Galamuka! Galamuka! Tavala mphamvu zako, Ziyoni; tavala zovala zako zokongola, Yerusalemu, mzinda wopatulika; pakuti kuyambira tsopano sadzalowanso kwa iwe wosadulidwa ndi wodetsedwa. Dzisanse fumbi; uka, khala tsonga, Yerusalemu; udzimasulire maunyolo a pakhosi pako, iwe mwana wamkazi wam'nsinga wa Ziyoni. Pakuti atero Yehova, Inu munagulitsidwa chabe, ndipo mudzaomboledwa opanda ndalama. Pakuti Ambuye Yehova atero, Anthu anga ananka ku Ejipito poyamba paja, kukakhala kumeneko; ndipo Asiriya anawatsendereza popanda chifukwa. Chifukwa chake kodi ndichitenji pano? Ati Yehova; popeza anthu anga achotsedwa popanda kanthu? Akuwalamulira awaliritsa, ati Yehova; ndipo dzina langa lichitidwa mwano tsiku lonse kosalekeza. Chifukwa chake anthu anga adzadziwa dzina langa; chifukwa chake tsiku limenelo iwo adzadziwa kuti Ine ndine amene ndinena; taonani, ndine pano. Ha, akongolatu pamapiri mapazi a iye amene adza ndi uthenga wabwino, amene abukitsa mtendere, amene adza ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino, amene abukitsa chipulumutso; amene ati kwa Ziyoni, Mulungu wako ndi mfumu. Mau a alonda ako! Akweza mau, aimba pamodzi; pakuti adzaona maso ndi maso, pamene Yehova abwerera kudza ku Ziyoni. Kondwani zolimba, imbani pamodzi, inu malo abwinja a pa Yerusalemu; pakuti Yehova watonthoza mtima wa anthu ake, waombola Yerusalemu. Yehova wavula mkono wake woyera pamaso pa amitundu onse; ndi malekezero onse a dziko lapansi adzaona chipulumutso cha Mulungu wathu. Chokani inu, chokani inu, tulukani ku Babiloni; musakhudze kanthu kodetsa; tulukani pakati pake, khalani okonzeka, inu amene munyamula zotengera za Yehova. Pakuti simudzachoka mofulumira, kapena kunka mothawa; pakuti Yehova adzakutsogolerani, ndi Mulungu wa Israele adzadikira pambuyo panu. Taonani, Mtumiki wanga adzachita mwanzeru; adzakwezedwa ndi kutukulidwa pamwamba, nadzakhala pamwambamwamba. Monga ambiri anazizwa ndi iwe Israele, momwemo nkhope yake yaipitsidwa ndithu, kupambana munthu aliyense, ndi maonekedwe ake kupambana ana a anthu; momwemonso Iye adzawazawaza mitundu yambiri; mafumu adzamtsekera Iye pakamwa pao; pakuti chimene sichinauzidwa kwa iwo adzachiona, ndi chimene iwo sanamve adzazindikira. Ndani wamvera uthenga wathu? Ndi mkono wa Yehova wavumbulukira yani? Pakuti ameneyo adzaphuka pamaso pake ngati mtengo wanthete, ndi ngati muzu womera m'nthaka youma; Iye alibe maonekedwe, pena kukongola; ndipo pamene timuona palibe kukongola kuti timkhumbe. Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu wombisira anthu nkhope zao; ndipo ife sitinamlemekeza. Zoonadi Iye ananyamula zowawa zathu, ndi kusenza zisoni zathu; koma ife tinamuyesa wokhomedwa, wokanthidwa ndi Mulungu, ndi wovutidwa. Koma Iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, natundudzidwa chifukwa cha mphulupulu zathu; chilango chotitengera ife mtendere chinamgwera Iye; ndipo ndi mikwingwirima yake ife tachiritsidwa. Tonse tasochera ngati nkhosa; tonse tayenda yense m'njira ya mwini yekha; ndipo Yehova anaika pa Iye mphulupulu ya ife tonse. Iye anatsenderezedwa koma anadzichepetsa yekha osatsegula pakamwa pake; ngati nkhosa yotsogoleredwa kukaphedwa, ndi ngati mwanawankhosa amene ali duu pamaso pa omsenga, motero sanatsegule pakamwa pake. Anachotsedwa ku chipsinjo ndi chiweruziro; ndipo ndani adzafotokoza nthawi ya moyo wake? Pakuti walikhidwa kunja kuno; chifukwa cha kulakwa kwa anthu anga Iye anakhomedwa. Ndipo anaika manda ake pamodzi ndi oipa, ndi pamodzi ndi olemera mu imfa yake, ngakhale Iye sanachite chiwawa, ndipo m'kamwa mwake munalibe chinyengo. Koma kunakomera Yehova kumtundudza; anammvetsa zowawa; moyo wake ukapereka nsembe yopalamula, Iye adzaona mbeu yake, adzatanimphitsa masiku ake; ndipo chomkondweretsa Yehova chidzakula m'manja mwake. Iye adzaona zotsatira mavuto a moyo wake, nadzakhuta nazo; ndi nzeru zake mtumiki wanga wolungama adzalungamitsa ambiri, nadzanyamula mphulupulu zao. Chifukwa chake ndidzamgawira gawo ndi akulu; ndipo adzagawana ndi amphamvu zofunkha; pakuti Iye anathira moyo wake kuimfa; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi olakwa; koma ananyamula machimo a ambiri, napembedzera olakwa. Imba, iwe wouma, amene sunabala; imba zolimba ndi kufuula zolimba, iwe amene sunabala mwana; pakuti ana a mfedwa achuluka koposa ana a mkazi wokwatibwa ndi mwamuna, ati Yehova. Kuza malo a hema wako, afunyulule zinsalu za mokhalamo iwe; usaleke, tanimphitsa zingwe zako, limbitsa zikhomo zako. Pakuti iwe udzafalikira ponse pa dzanja lamanja ndi lamanzere, ndipo mbeu yako idzalandira amitundu cholowa chao, ndi kukhalitsa anthu m'mabwinja. Usaope, pakuti sudzakhala ndi manyazi; usasokonezedwe, pakuti sudzachitidwa manyazi; pakuti udzaiwala manyazi a ubwana wako, ndi chitonzo cha umasiye wako sudzachikumbukiranso. Pakuti Mlengi wako ndiye mwamuna wako; Yehova wa makamu ndiye dzina lake; ndi Woyera wa Israele ndiye Mombolo wako; Iye adzatchedwa Mulungu wa dziko lonse lapansi. Pakuti Yehova wakuitana iwe monga mkazi wakusiyidwa ndi wosauka m'mzimu, ngakhale mkazi wa ubwana wochotsedwa, ati Mulungu wako. Kamphindi kakang'ono ndakusiya iwe, koma ndi chifundo chambiri ndidzakusonkhanitsa. M'kukwiya kwa kusefukira ndinakubisira nkhope yanga kamphindi; koma ndi kukoma mtima kwa chikhalire ndidzakuchitira chifundo, ati Yehova Mombolo wako. Pakuti kumeneku kuli kwa Ine monga madzi a Nowa; pakuti monga ndinalumbira kuti madzi a Nowa sadzamizanso pa dziko lapansi, momwemo ndinalumbira kuti sindidzakukwiyira iwe, pena kukudzudzula. Pakuti mapiri adzachoka, ndi zitunda zidzasunthika; koma kukoma mtima kwanga sikudzakuchokera iwe, kapena kusunthika chipangano changa cha mtendere, ati Yehova amene wakuchitira iwe chifundo. Iwe wosautsidwa, wobelukabeluka ndi namondwe, wosatonthola mtima, taona, ndidzakhazika miyala yako m'mawangamawanga abwino, ndi kukhazika maziko ako ndi masafiro. Ndipo ndidzamanga mazenera ako ndi miyala yofiira, ndi zipata zako ndi bareketi, ndi malire ako onse ndi miyala yokondweretsa. Ndipo ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu. M'chilungamo iwe udzakhazikitsidwa, udzakhala kutali ndi chipsinjo, pakuti sudzaopa; udzakhala kutali ndi mantha, pakuti sadzafika chifupi ndi iwe. Taona, iwo angasonkhanitse pamodzi, koma si ndi Ine; amene aliyense adzasonkhana pamodzi akangane ndi iwe adzagwa chifukwa cha iwe. Taona, ndalenga wachipala amene avukuta moto wamakala, ndi kutulutsamo chida cha ntchito yake; ndipo ndalenga woononga kuti apasule. Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m'chiweruzo udzalitsutsa. Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova, ndi chilungamo chao chimene chifuma kwa Ine, ati Yehova. Inu nonse, inu akumva ludzu, idzani kumadzi; ndi osowa ndalama idzani inu mugule mudye; inde idzani, mugule vinyo ndi mkaka opanda ndalama ndi opanda mtengo wake. Bwanji inu mulikutayira ndalama chinthu chosadya, ndi kutayira malipiro anu zosakhutitsa? Mverani Ine mosamalitsa, nimudye chimene chili chabwino, moyo wanu nukondwere ndi zonona. Tcherani khutu lanu, mudze kwa Ine, imvani, mzimu wanu nudzakhala ndi moyo; ndipo ndidzapangana nanu chipangano chosatha, ndicho zifundo zoona za Davide. Taonani, ndampereka iye akhale mboni ya anthu, wotsogolera ndi wolamulira anthu. Taona, iwe udzaitana mtundu umene sunaudziwa, ndi mtundu umene sunakudziwa udzakuthamangira, chifukwa cha Yehova Mulungu wako, ndi chifukwa cha Woyera wa Israele; pakuti Iye wakukometsa. Funani Yehova popezeka Iye, itanani Iye pamene ali pafupi; woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamchitira chifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti Iye adzakhululukira koposa. Pakuti maganizo anga sali maganizo anu, ngakhale njira zanu sizili njira zanga, ati Yehova. Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga zili zazitali kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu. Pakuti monga mvula imagwa pansi ndi matalala, kuchokera kumwamba yosabwerera komweko, koma ikhamiza nthaka ndi kuibalitsa, ndi kuiphukitsa, ndi kuipatsitsa mbeu kwa wobzala, ndi chakudya kwa wakudya; momwemo adzakhala mau anga amene atuluka m'kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula m'mene ndinawatumizira. Pakuti inu mudzatuluka ndi kukondwa, ndi kutsogozedwa ndi mtendere; mapiri ndi zitunda, zidzaimba zolimba pamaso panu, ndi mitengo yonse ya m'thengo idzaomba m'manja mwao. M'malo mwa mithethe mudzatuluka mtengo wamlombwa; ndi m'malo mwa lunguzi mudzamera mtengo wamchisu; ndipo chidzakhala kwa Yehova ngati mbiri, ngati chizindikiro chosatha, chimene sichidzalikhidwa. Atero Yehova, Sungani inu chiweruziro, ndi kuchita chilungamo; pakuti chipulumutso changa chili pafupi kudza, ndi chilungamo changa chili pafupi kuti chivumbulutsidwe. Wodala munthu amene achita ichi, ndi mwana wa munthu amene agwira zolimba ichi, amene asunga Sabata osaliipitsa, nasunga dzanja lake osachita nalo choipa chilichonse. Mlendo amene wadziphatika yekha kwa Yehova asanene, kuti, Yehova adzandilekanitsa ndithu ndi anthu ake; pena mfule asanene, Taonani ine ndili mtengo wouma. Pakuti atero Yehova kwa mifule imene isunga masabata, nisankha zinthu zimene zindikondweretsa Ine, nigwira zolimba chipangano changa, Kwa iyo ndidzapatsa m'nyumba yanga ndi m'kati mwa makoma anga malo, ndi dzina loposa la ana aamuna ndi aakazi; ndidzawapatsa dzina lachikhalire limene silidzadulidwa. Alendonso amene adziphatika okha kwa Yehova, kuti amtumikire Iye, ndi kukonda dzina la Yehova, akhale atumiki ake, yense amene asunga sabata osaliipitsa, nagwira zolimba chipangano changa; naonso ndidzanka nao kuphiri langa lopatulika, ndi kuwasangalatsa m'nyumba yanga yopemphereramo; zopereka zao zopsereza ndi nsembe zao zidzalandiridwa pa guwa la nsembe langa; pakuti nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo anthu onse. Ambuye Yehova amene asonkhanitsa otayika a Israele ati, Komabe ndidzasonkhanitsa ena kwa iye, pamodzi ndi osonkhanitsidwa akeake. Inu zilombo zonse za m'thengo, idzani kulusa, inde zilombo inu nonse za m'nkhalango. Alonda ake ali akhungu, iwo onse ali opanda nzeru; iwo onse ali agalu achete, osatha kuuwa; kungolota, kugona pansi, kukonda kugona tulo. Inde agalu ali osusuka, sakhuta konse; amenewa ali abusa osazindikira; iwo onse atembenukira kunjira zao, yense kutsata phindu lake m'dera lake. Idzani inu, ati iwo, ndidzatengera vinyo, ndipo tidzakhuta chakumwa chaukali; ndipo mawa kudzakhala monga tsiku lalero, tsiku lalikulu loposa ndithu. Wolungama atayika, ndipo palibe munthu wosamalirapo; ndipo anthu achifundo atengedwa, palibe wolingalira kuti wolungama achotsedwa pa choipa chilinkudza. Iye alowa mumtendere, iwo apuma pa mphasa zao, yense woyenda moongoka. Koma sendererani kuno chifupi, inu ana amuna a watsenga, mbeu yachigololo ndi yadama. Ndiye yani mudzikondweretsa momseka? Ndani mulikumyasamira kukamwa, ndi kumtulutsira lilime? Kodi inu simuli ana akulakwa, mbeu yonama? Inu amene muutsa zilakolako zanu pakati pa mathundu, patsinde pa mitengo yonse ya gudugudu, amene mupha ana m'zigwa pansi pa mapanga a matanthwe? Pakuti pa miyala yosalala ya m'chigwa pali gawo lako; iyo ndiyo gawo lako; ndiyo imene unaitsanulirira nsembe yothira, ndi kupereka nsembe yaufa. Kodi ndidzapembedzedwa pa zinthu zimenezi? Pamwamba pa phiri lalitalitali unayala mphasa yako; kumenekonso wakwera kukapereka nsembe. Ndi kumbuyo kwa zitseko ndi mphuthu waimiritsa chikumbutso chako, pakuti wadzionetsa wekha kwa wina, wosati kwa Ine; ndipo wakwerako, wakuza mphasa yako, ndi kupangana nao pangano; unakonda mphasa yao kumene unaiona. Ndipo unanka kwa mfumu, utadzola mafuta ndi kuchulukitsa zonunkhira zako; ndipo unatumiza atumwi ako kutali; ndipo wadzichepetsa wekha kufikira kunsi kumanda. Unatopa ndi njira yako yaitali; koma sunanene, Palibe chiyembekezo; iwe wapeza moyo wa dzanja lako; chifukwa chake sunalefuka. Ndipo ndi yani amene wamuopa ndi kuchita naye mantha, kuti wanama, osandikumbukira Ine, kapena kundisamalira? Kodi Ine sindinakhala chete nthawi yambiri, ndipo iwe sunandiopa Ine konse? Ndidzaonetsa chilungamo chako ndi ntchito zako sudzapindula nazo. Pamene pakufuula iwe akupulumutse amene unawasonkhanitsa; koma mphepo idzawatenga, mpweya udzachotsa onse; koma iye amene andikhulupirira Ine adzakhala ndi dziko, nadzakhala nacho cholowa m'phiri langa lopatulika. Ndipo adzanena, Undani, undani, konzani njira, chotsani chokhumudwitsa m'njira mwa anthu anga. Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo atali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka. Pakuti sindidzatsutsana kunthawi zonse, sindidzakwiya masiku onse; pakuti mzimu udzalefuka pamaso pa Ine, ndi miyoyo imene ndinailenga. Chifukwa cha kuipa kwa kusirira kwake ndinakwiya ndi kummenya iye; ndinabisa nkhope yanga, ndipo ndinakwiya; ndipo iye anankabe mokhota m'njira ya mtima wake. Ndaona njira zake, ndipo ndidzamchiritsa; ndidzamtsogoleranso, ndi kumbwezera iye ndi olira maliro ake zotonthoza mtima. Ndilenga chipatso cha milomo, Mtendere, mtendere kwa iye amene ali kutali, ndi kwa iye amene ali chifupi, ati Yehova; ndipo ndidzamchiritsa iye. Koma oipa ali ofanana ndi nyanja yowinduka; pakuti siingapume, ndi madzi ake autsa matope ndi uve. Palibe mtendere, ati Mulungu wanga, kwa oipa. Fuula zolimba, usalekerere, kweza mau ako ngati lipenga, ndi kuwafotokozera anthu anga cholakwa chao, ndi banja la Yakobo machimo ao. Koma iwo andifuna Ine tsiku ndi tsiku, ndi kukondwera kudziwa njira zanga; monga mtundu wa anthu ochita chilungamo, osasiya chilangizo cha Mulungu wao, iwo andipempha Ine zilangizo zolungama, nakondwerera kuyandikira kwa Mulungu. Amati, Bwanji ife tasala kudya, ndipo Inu simuona? Ndi bwanji ife tavutitsa moyo wathu, ndipo Inu simusamalira? Taonani, tsiku la kusala kudya kwanu inu mupeza kukondwerera kwanu, ndi kutsendereza antchito anu onse. Taonani, inu musala kudya kuti mukangane ndi kutsutsana ndi kukantha ndi nkhonya yoipa; inu simusala kudya tsiku lalero kuti mumveketse mau anu kumwamba. Kodi kusala kudya koteroko ndiko ndinakusankha? Tsiku lakuvutitsa munthu moyo wake? Kodi ndiko kuweramitsa mutu wake monga bango, ndi kuyala chiguduli ndi phulusa pansi pake? Kodi uyesa kumeneko kusala kudya, ndi tsiku lovomerezeka kwa Yehova? Kodi kumeneku si kusala kudya kumene ndinakusankha: kumasula nsinga za zoipa, ndi kumasula zomanga goli, ndi kuleka otsenderezedwa amuke mfulu, ndi kuti muthyole magoli onse? Kodi si ndiko kupatsa chakudya chako kwa anjala, ndi kuti ubwere nao kunyumba kwako aumphawi otayika? Pakuona wamaliseche kuti umveke, ndi kuti usadzibisire wekha a chibale chako? Pomwepo kuunika kwako kudzawalitsa monga m'mawa, ndi kuchira kwako kudzaonekera msangamsanga; ndipo chilungamo chako chidzakutsogolera; ulemerero wa Yehova udzakhala wotchinjiriza pambuyo pako. Pamenepo udzaitana, ndipo Yehova adzayankha; udzafuula ndipo Iye adzati, Ndine pano. Ngati uchotsa pakati pa iwe goli, kukodolana moipa, ndi kulankhula moipa, ndipo ngati upereka kwa wanjala chimene moyo wako umakhumba, ndi kukhutitsa moyo wovutidwa, pomwepo kuunika kwako kudzauka mumdima, ndipo usiku wako udzanga usana; ndipo Yehova adzakutsogolera posalekai, ndi kukhutitsa moyo wako m'chilala, ndi kulimbitsa mafupa ako; ndipo udzafanana ndi munda wothirira madzi, ndi kasupe wamadzi amene madzi ake saphwa konse. Ndipo iwo amene adzakhala a iwe adzamanga malo akale abwinja; udzautsa maziko a mibadwo yambiri; udzatchedwa Wokonza pogumuka, Wakubwezera njira zakukhalamo. Ukaletsa phazi lako pa Sabata, ndi kusiya kuchita kukondwerera kwako tsiku langa lopatulika, ndi kuyesa Sabata tsiku lokondwa lopatulika la Yehova, lolemekezeka, ndipo ukalilemekeza ilo, osachita njira zako zokha, osafuna kukondwa kwako kokha, osalankhula mau ako okha; pomwepo udzakondwa mwa Yehova; ndipo Ine ndidzakuyendetsa pa misanje ya dziko lapansi; ndipo ndidzakudyetsa cholowa cha kholo lako Yakobo; pakuti pakamwa pa Yehova pananenapo. Taonani, mkono wa Yehova sufupika, kuti sungathe kupulumutsa; khutu lake silili logontha, kuti silingamve; koma zoipa zanu zakulekanitsani inu ndi Mulungu wanu; ndipo machimo anu abisa nkhope yake kwa inu, kuti Iye sakumva. Pakuti manja anu adetsedwa ndi mwazi, ndi zala zanu ndi mphulupulu, milomo yanu yanena zonama, lilime lanu lilankhula moipa. Palibe wotulutsa mlandu molungama, ndipo palibe wonena zoona; iwo akhulupirira mwachabe, nanena zonama; iwo atenga kusaweruzika ndi kubala mphulupulu. Iwo afungatira mazira a mphiri aswetse, naluka ukonde wa kangaude; iye amene adya mazira ake amafa, ndi choswanyikacho chisweka nichikhala songo. Maukonde ao sadzakhala zovala, sadzafunda ntchito zao; ntchito zao zili ntchito zoipa, ndi chiwawa chili m'manja mwao. Mapazi ao athamangira koipa, ndipo iwo afulumira kukhetsa mwazi wosachimwa; maganizo ao ali maganizo oipa; bwinja ndi chipasuko zili m'njira mwao. Njira ya mtendere saidziwa, ndipo palibe chiweruziro m'mayendedwe mwao; akhotetsa njira zao; aliyense ayenda m'menemo sadziwa mtendere. Chifukwa chake chiweruziro chili patali ndi ife, ndi chilungamo sichitipeza; tiyang'anira kuunika, koma taona mdima; tiyang'anira kuyera, koma tiyenda m'usiku. Tiyambasira khoma ngati wakhungu, inde tiyambasa monga iwo opanda maso; tiphunthwa usana monga m'chizirezire; tili m'malo amdima ngati akufa. Tonse tibangula ngati zilombo, ndi kulira maliro zolimba ngati nkhunda; tiyang'anira chiweruziro koma palibe; tiyang'anira chipulumutso koma chili patali ndi ife. Pakuti zolakwa zathu zachuluka pamaso pa Inu, ndipo machimo athu atineneza ife; pakuti zolakwa zathu zili ndi ife, ndipo zoipa zathu tizidziwa; ndizo kulakwabe ndi kukanabe Yehova, ndi kuleka kutsata Mulungu wathu; kulankhula zotsendereza ndi kupanduka, kuganizira ndi kunena pakamwa mau akunyenga otuluka mumtima. Ndipo chiweruziro chabwerera m'mbuyo, ndi chilungamo chaima patali; pakuti choona chagwa m'khwalala, ndi kuongoka sikungalowe. Inde choona chisoweka; iye amene asiya choipa, zifunkhidwa zake; ndipo Yehova anaona ichi, ndipo chidamuipira kuti palibe chiweruzo. Ndipo Iye anaona kuti palibe munthu, nazizwa kuti palibe wopembedzera; chifukwa chake mkono wakewake unadzitengera yekha chipulumutso; ndi chilungamo chake chinamchirikiza. Ndipo anavala chilungamo monga chida chapachifuwa, ndi chisoti cha chipulumutso pamutu pake; navala zovala zakubwezera chilango, navekedwa ndi changu monga chofunda. Monga mwa ntchito zao momwemo Iye adzabwezera adani ake chilango; nadzabwezeranso zisumbu chilango. Chomwecho iwo adzaopa dzina la Yehova kuchokera kumadzulo, ndi ulemerero wake kumene kutulukira dzuwa; pakuti pamene mdani adzafika ngati chigumula, mzimu wa Yehova udzamkwezera mbendera yomletsa. Ndipo Mombolo adzafika ku Ziyoni, ndi kwa iwo amene atembenuka kusiya kulakwa mwa Yakobo, ati Yehova. Ndipo kunena za Ine, ili ndi pangano langa ndi iwo, ati Yehova; mzimu wanga umene uli pa iwe, ndi mau anga amene ndaika m'kamwa mwako sadzachoka m'kamwa mwako, pena m'kamwa mwa ana ako, pena m'kamwa mwa mbeu ya mbeu yako, ati Yehova, kuyambira tsopano ndi kunthawi zonse. Nyamuka, wala, pakuti kuunika kwako kwafika, ndi ulemerero wa Yehova wakutulukira. Pakuti taona, mdima udzaphimba dziko lapansi, ndi mdima wa bii mitundu ya anthu; koma Yehova adzakutulukira ndi ulemerero wake udzaoneka pa iwe. Ndipo amitundu adzafika kwa kuunika kwako, ndi mafumu kwa kuyera kwa kutuluka kwako. Tukula maso ako uunguzeunguze ndi kuona; iwo onse asonkhana pamodzi, adza kwa iwe; ana ako amuna adzachokera kutali, ndi ana ako akazi adzaleredwa pambali. Pamenepo udzaona ndi kuunikidwa, ndipo mtima wako udzanthunthumira ndi kukuzidwa; pakuti unyinji wa nyanja udzakutembenukira, chuma cha amitundu chidzafika kwa iwe. Gulu la ngamira lidzakukuta, ngamira zazing'ono za Midiyani ndi Efa; iwo onsewo adzachokera ku Sheba adzabwera nazo golide ndi lubani; ndipo adzalalikira matamando a Yehova. Zoweta za Kedara zidzasonkhana kwa iwe, nkhosa zamphongo za Nebayoti zidzakutumikira; izo zidzafika ndi kulandiridwa pa guwa langa la nsembe; ndipo ndidzakometsa nyumba ya ulemerero wanga. Ndani awa amene auluka ngati mtambo, ndi monga nkhunda kumazenera ao? Zoonadi, zisumbu zidzandilindira Ine; zidzayamba ndi ngalawa za Tarisisi kutenga ana ako amuna kutali, golide wao ndi siliva wao pamodzi nao, chifukwa cha dzina la Yehova Mulungu wako, ndi chifukwa cha Woyera wa Israele, popeza Iye wakukometsa iwe. Ndipo alendo adzamanga malinga ako, ndi mafumu ao adzakutumikira; pakuti m'kukwiya kwanga ndinakantha, koma mokomera mtima ndidakuchitira iwe chifundo. Zipata zako zidzakhalabe zotseguka, sizidzatsekedwa usana pena usiku, kuti abwere nacho kwa iwe chuma cha amitundu, ndi mafumu ao otsogozedwa nao pamodzi. Pakuti mtundu ndi ufumu umene udzakana kukutumikira udzaonongeka; inde mitundu imeneyo idzasakazidwa ndithu. Ulemerero wa Lebanoni udzafika kwa iwe; mtengo wamlombwa, mtengo wamkuyu ndi mtengo wanaphini pamodzi, kukometsera malo a Kachisi wanga; ndipo ndidzachititsa malo a mapazi anga ulemerero. Ndipo ana amuna a iwo amene anavuta iwe adzafika, nadzakugwadira; ndipo iwo onse amene anakuchepetsa iwe adzagwadira kumapazi ako, nadzakutcha iwe, Mudzi wa Yehova, Ziyoni wa Woyera wa Israele. Ungakhale unasiyidwa ndi kudedwa, osapita munthu mwa iwe, Ine ndidzakusandutsa changwiro chosatha, chokondweretsa cha mibadwo yambiri. Iwe udzayamwanso mkaka wa amitundu, nudzayamwa bere la mafumu, nudzadziwa kuti Ine Yehova ndine Mpulumutsi wako, ndi Mombolo wako, Wamphamvu ya Yakobo. M'malo mwa mkuwa ndidzatenga golide, ndi m'malo mwa chitsulo ndidzatenga siliva, ndi m'malo mwa mtengo ndidzatenga mkuwa, ndi m'malo mwa miyala ndidzatenga chitsulo; ndidzakuikira akapitao a mtendere, ndi oyang'anira ntchito a chilungamo. Chiwawa sichidzamvekanso m'dziko mwako, kupululutsa pena kupasula m'malire ako; koma udzatcha malinga ako Chipulumutso, ndi zipata zako Matamando. Dzuwa silidzakhalanso kuunika kwako usana, ngakhale mwezi sudzakuunikiranso kuti kuyere; koma Yehova adzakhala kwa iwe kuunika kosatha, ndi Mulungu wako adzakhala ulemerero wako. Dzuwa lako silidzalowanso, mwezi wako sudzanka kumidima; pakuti Yehova adzakhala kuunika kwako kosatha, ndi masiku a kulira maliro ako adzatha. Anthu ako adzakhalanso onse olungama; dzikolo lidzakhala cholowa chao kunthawi zonse, nthambi yooka Ine, ntchito ya manja anga, kuti Ine ndikuzidwe. Wamng'ono adzasanduka chikwi, ndi wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu; Ine Yehova ndidzafulumiza ichi m'nthawi yake. Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende; ndikalalikire chaka chokomera Yehova, ndi tsiku lakubwezera la Mulungu wathu; ndikatonthoze mtima wa onse amene akulira maliro; ndikakonzere iwo amene alira maliro m'Ziyoni, ndi kuwapatsa chovala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, chovala cha matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo atchedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe. Ndipo iwo adzamanga mabwinja akale, nadzamanga pa miunda yakale, nadzakonzanso midzi yopasuka, mabwinja a mibadwo yambiri. Ndipo alendo adzaimirira ndi kudyetsa magulu ako, ndi anthu akunja adzakhala olima ako, ndi kukukonzera minda yamphesa. Koma inu mudzatchedwa ansembe a Yehova; anthu adzakuyesani inu atumiki a Mulungu wathu; inu mudzadya chuma cha amitundu, nimudzalowa mu ulemerero wao. M'malo mwa manyazi anu, owirikiza; ndi chitonzo iwo adzakondwera ndi gawo lao; chifukwa chake iwo adzakhala nacho m'dziko mwao cholowa chowirikiza, adzakhala nacho chikondwerero chosatha. Pakuti Ine Yehova ndikonda chiweruziro, ndida chifwamba ndi choipa; ndipo ndidzawapatsa mphotho yao m'zoonadi; ndipo ndidzapangana nao pangano losatha. Ndipo ana ao adzadziwidwa mwa amitundu, ndi obadwa ao mwa anthu; onse amene awaona adzawazindikira kuti iwo ndiwo ana amene Yehova wadalitsa. Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Ine wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo. Pakuti monga dziko liphukitsa mphundu zake, ndi monga munda umeretsa zobzalamo, momwemo Ambuye Yehova adzaphukitsa chilungamo ndi matamando pamaso pa amitundu onse. Chifukwa cha Ziyoni sindidzakhala chete, ndi chifukwa cha Yerusalemu sindidzapuma, kufikira chilungamo chake chidzatuluka monga kuyera, ndi chipulumutso chake monga nyali yoyaka. Ndipo amitundu adzaona chilungamo chako, ndi mafumu onse ulemerero wako; ndipo udzatchedwa dzina latsopano, limene m'kamwa mwa Yehova mudzatchula. Iwe udzakhalanso korona wokongola m'dzanja la Yehova, korona wachifumu m'dzanja la Mulungu wako. Iwe sudzatchedwanso Wosiyidwa; dziko lako silidzatchedwanso Bwinja; koma iwe udzatchedwa Hefiziba ndi dziko lako Beula; pakuti Yehova akondwera mwa iwe, ndipo dziko lako lidzakwatiwa. Pakuti monga mnyamata akwatira namwali, momwemo ana ako amuna adzakukwatira iwe; ndi monga mkwati akondwera ndi mkwatibwi, momwemo Mulungu wako adzakondwera nawe. Ndaika alonda pa malinga ako, Yerusalemu; iwo sadzakhala chete usana pena usiku; inu akukumbutsa Yehova musakhale chete, ndipo musamlole akhale chete, kufikira Iye atakhazikitsa naika Yerusalemu akhale tamando m'dziko lapansi. Yehova analumbira pa dzanja lake lamanja, ndi mkono wake wamphamvu, Zoonadi, sindidzaperekanso tirigu wako akhale chakudya cha adani ako, ndipo alendo sadzamwa vinyo wako amene iwe unagwirira ntchito; koma iwo amene adzakolola adzadya ndi kutamanda Yehova; ndi iwo amene adzamtchera adzamumwa m'mabwalo a Kachisi wanga. Pitani, pitani pazipata; konzani njira ya anthu; undani, undani khwalala; chotsani miyala, kwezani mbendera ya anthu. Taonani, Yehova walalikira kufikira malekezero a dziko lapansi. Nenani kwa mwana wamkazi wa Ziyoni, Taona chipulumutso chako chifika; taona mphotho yake ali nayo, ndi ntchito yake ili pamaso pake. Ndipo iwo adzawatcha Anthu opatulika, Oomboledwa a Yehova; ndipo iwe udzatchedwa Wofunidwa, Mudzi wosasiyidwa. Ndani uyu alikudza kuchokera ku Edomu, ndi zovala zonika zochokera ku Bozira? Uyu wolemekezeka m'chovala chake, nayenda mu ukulu wa mphamvu zake? Ndine amene ndilankhula m'cholungama, wa mphamvu yakupulumutsa. Chophimba chako chifiiriranji, ndi zovala zako zifanana bwanji ndi woponda mopondera mphesa? Ndaponda ndekha mopondera mphesa, ndipo panalibe nane mmodzi wa mitundu ya anthu; inde ndinawaponda m'kukwiya kwanga, ndi kuwapondereza mu ukali wanga; ndi mwazi wa moyo wao unawazidwa pa zovala zanga; ndipo ndadetsa chofunda changa chonse. Pakuti tsiku lakubwezera lili mumtima mwanga, ndi chaka cha kuombola anthu anga chafika. Ndipo ndinayang'ana, koma panalibe wothangata; ndipo ndinadabwa kuti panalibe wochirikiza; chifukwa chake mkono wangawanga unanditengera chipulumutso, ndi ukali wanga unandichirikiza Ine. Ndipo ndinapondereza anthu m'kukwiya kwanga, ndi kuwatswanya mu ukali wanga, ndi kutsanulira mwazi wa moyo wao. Ndidzatchula zachifundo chake cha Yehova, ndi matamando a Yehova, monga mwa zonse zimene Yehova wapereka kwa ife; ndi ubwino wake waukulu kwa banja la Israele, umene Iye wapereka kwa iwo, monga mwa chifundo chake, ndi monga mwa ntchito zochuluka za chikondi chake. Pakuti anati, Zoonadi iwo ndiwo anthu anga, ana amene sangachite monyenga; chomwecho Iye anali Mpulumutsi wao. M'mazunzo ao onse Iye anazunzidwa, ndipo mthenga wakuimirira pamaso pake anawapulumutsa; m'kukonda kwake ndi m'chisoni chake Iye anawaombola, nawabereka nawanyamula masiku onse akale. Koma iwo anapandukira ndi kumvetsa chisoni mzimu wake woyera, chifukwa chake Iye anasandulika mdani wao, nawathira nkhondo Iye yekha. Pamenepo iwo anakumbukira masiku akale, Mose ndi anthu ake, nati, Ali kuti Iye amene anawatulutsa m'nyanja pamodzi ndi abusa a gulu lake? Ali kuti Iye amene anaika mzimu wake woyera pakati pao, amene anayendetsa mkono wake waulemerero pa dzanja lamanja la Mose? Amene anagawanitsa madzi pamaso pao, kuti adzitengere mbiri yosatha? Amene anawatsogolera kupitira mwa kuya monga kavalo m'chipululu osaphunthwa iwo? Monga ng'ombe zotsikira kuchigwa mzimu wa Yehova unawapumitsa; chomwecho inu munatsogolera anthu anu kudzitengera mbiri yaulemerero. Tayang'anani kunsi, taonani pokhala panu poyera, ndi pa ulemerero wanu, changu chanu ndi ntchito zanu zamphamvu zili kuti? Mwanditsekerezera zofunafuna za mtima wanu ndi chisoni chanu. Pakuti Inu ndinu Atate wathu, ngakhale Abrahamu satidziwa ife, ndi Israele satizindikira ife. Inu Yehova ndinu Atate wathu, Mombolo wathu wachikhalire ndi dzina lanu. Yehova bwanji mwatisocheretsa kusiya njira zanu, ndi kuumitsa mitima yathu tisakuopeni? Bwerani, chifukwa cha atumiki anu, mafuko a cholowa chanu. Anthu anu opatulika anakhala nacho kanthawi kokha; adani athu apondereza Kachisi wanu wopatulika. Ife takhala ngati iwo amene simunawalamulira konse, ngati iwo amene sanatchedwe dzina lanu. Mwenzi mutang'amba kumwamba ndi kutsikira pansi, kuti mapiri agwedezeke pamaso panu; monga pamene moto uyatsa zitsamba, ndi moto uwiritsa madzi; kudziwitsa kwa amaliwongo anu dzina lanu, kuti amitundu anthunthumire pamaso panu. Pamene Inu munachita zinthu zoopsa, zimene ife sitinayang'anira, Inu munatsika, mapiri anagwedezeka pamaso panu. Pakuti kuyambira kale anthu sanamve pena kumvetsa ndi khutu, ngakhale diso silinaone Mulungu wina popanda Inu, amene amgwirira ntchito iye amene amlindirira Iye. Inu mukomana ndi iye amene akondwerera, nachita chilungamo, iwo amene akumbukira Inu m'njira zanu; taonani Inu munakwiya, ndipo ife tinachimwa; takhala momwemo nthawi yambiri, kodi tidzapulumutsidwa? Pakuti ife tonse takhala ngati wina amene ali wosakonzeka; ndi zolungama zathu zonse zili ngati chovala chodetsedwa; ndipo ife tonse tifota monga tsamba, ndi zoipa zathu zitiuluza monga mphepo. Ndipo palibe amene aitana dzina lanu, amene adzikakamiza yekha kugwiritsa Inu; pakuti Inu mwatibisira nkhope yanu, ndipo mwatinyeketsa ndi zoipa zathu. Koma tsopano, Yehova, Inu ndinu Atate wathu; ife tili dongo, ndipo Inu ndinu Muumbi wathu; ndipo ife tonse tili ntchito ya dzanja lanu. Musakwiye kopambana, Yehova, musakumbukire zoipa nthawi zonse; taonani, yang'anani ife, tikupembedzani Inu, ife tonse tili anthu anu. Midzi yanu yopatulika yasanduka chipululu, Ziyoni wasanduka chipululu, Yerusalemu wasanduka bwinja. Nyumba yathu yopatulika ndi yokongola, m'mene makolo athu anakutamandani Inu, yatenthedwa ndi moto; ndi zinthu zathu zonse zokondweretsa zapasuka. Kodi mudzadziletsa pa zinthuzi, Yehova? Kodi Inu mudzakhala chete ndi kutivutitsa ife zolimba? Iwo amene sanafunse za Ine andifunafuna; ndi iwo amene sanandipwaire andipeza; ndinati, Taonani Ine, taonani Ine, kwa mtundu umene sunatchula dzina langa. Ndatambasulira manja anga tsiku lonse kwa anthu opanduka, amene ayenda m'njira mosati mwabwino, kutsata maganizo aoao; anthu amene andiputa Ine kumaso kwanga nthawi zonse, apereka nsembe m'minda, nafukizira zonunkhira panjerwa; amene akhala pakati pa manda, ndi kugona m'malo am'tseri; amene adya nyama ya nkhumba, ndi msuzi wa zinthu zonyansa uli m'mbale zao; amene ati, Ima pa wekha, usadze chifupi ndi ine, pakuti ine ndili woyera kupambana iwe; amenewa ndiwo utsi m'mphuno mwanga, moto woyaka tsiku lonse. Taonani, chalembedwa pamaso panga; sindidzakhala chete, koma ndidzabwezera, inde ndidzabwezera pa chifuwa chao, zoipa zanuzanu pamodzi ndi zoipa za makolo anu, ati Yehova, amene anafukiza zonunkhira pamapiri, nandichitira mwano pazitunda; chifukwa chake Ine ndidzayesa ntchito yao yakale ilowe pa chifuwa chao. Atero Yehova, Monga vinyo watsopano apezedwa m'tsango, ndipo wina ati, Usaliononge, pakuti muli mdalitso m'menemo, ndidzachita chifukwa cha atumiki anga, kuti ndisawaononge onse. Ndipo ndidzatulutsa mbeu mwa Yakobo, ndi mwa Yuda wolowa nyumba wa mapiri anga; ndipo osankhidwa anga adzalandira cholowa chao, ndi atumiki anga adzakhala kumeneko. Ndipo Saroni adzakhala podyetsera nkhosa, ndi chigwa cha Akori chidzakhala pogona zoweta kwa anthu anga amene andifuna Ine. Koma inu amene mwasiya Yehova, amene mwaiwala phiri langa lopatulika, ndi kukonzera mulungu wamwai gome, ndi kudzazira mulungu waimfa zikho za vinyo wosanganiza; ndidzasankhiratu inu kulupanga, ndipo inu nonse mudzagwada ndi kuphedwa; pakuti pamene ndinaitana, inu simunayankhe; pamene ndinanena, simunamve; koma munachita choipa m'maso mwanga, ndi kusankha chimene Ine sindinakondwera nacho. Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taonani atumiki anga adzadya, koma inu mudzakhala ndi njala; taonani, atumiki anga adzamwa, koma inu mudzakhala ndi ludzu; taonani, atumiki anga adzasangalala, koma inu mudzakhala ndi manyazi; taonani, atumiki anga adzaimba ndi mtima wosangalala, koma inu mudzalira ndi mtima wachisoni; ndipo mudzafuula chifukwa cha kusweka mzimu. Ndipo mudzasiya dzina lanu likhale chitemberero kwa osankhidwa anga, ndipo Ambuye Yehova adzakupha iwe, nadzatcha atumiki ake dzina lina; chomwecho iye amene adzidalitsa yekha m'dziko lapansi, adzadzidalitsa yekha mwa Mulungu woona; ndipo iye amene alumbira m'dziko lapansi adzalumbira pa Mulungu woona; popeza zovuta zoyamba zaiwalika, ndi popeza zabisalika kumaso kwanga. Pakuti taonani, ndilenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima. Koma khalani inu okondwa ndi kusangalala kunthawi zonse ndi ichi ndichilenga; pakuti taonani, ndilenga Yerusalemu wosangalala, ndi anthu ake okondwa. Ndipo ndidzasangalala m'Yerusalemu, ndi kukondwera mwa anthu anga; ndipo mau akulira sadzamvekanso mwa iye, pena mau akufuula. Sipadzakhalanso khanda la masiku, pena munthu wokalamba osakwanitsa masiku ake; pakuti mwana adzafa wa zaka zana limodzi; ndipo wochimwa pokhala wa zaka zana limodzi adzatemberedwa. Ndipo iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzaoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzaoka, ndi wina kudya; pakuti monga masiku a mtengo adzakhala masiku a anthu anga; ndi osankhidwa anga adzasangalala nthawi zambiri ndi ntchito za manja ao. Iwo sadzagwira ntchito mwachabe, pena kubalira tsoka; pakuti iwo ndiwo mbeu ya odalitsidwa a Yehova, ndi obadwa ao adzakhala pamodzi ndi iwo. Ndipo padzakhala kuti iwo asanaitane Ine, ndidzayankha; ndipo ali chilankhulire, Ine ndidzamva. Mmbulu ndi mwanawankhosa zidzadyera pamodzi; ndi mkango udzadya udzu ngati ng'ombe; ndi fumbi lidzakhala chakudya cha njoka; sizidzapwetekana, kapena kusakazana m'phiri langa lonse lopatulika, ati Yehova. Atero Yehova, Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu, ndi dziko lapansi ndi choikapo mapazi anga; mudzandimangira Ine nyumba yotani? Ndi malo ondiyenera kupumamo ali kuti? Pakuti zonsezi mkono wanga wazilenga, momwemo zonsezi zinaoneka, ati Yehova; koma ndidzayang'anira munthu uyu amene ali waumphawi, ndi wa mzimu wosweka, nanthunthumira ndi mau anga. Wakupha ng'ombe alingana ndi wakupha munthu; iye wapereka nsembe ya mwanawankhosa alingana ndi wothyola khosi la galu; wothira nsembe yaufa akunga wothira mwazi wa nkhumba; wofukiza lubani akunga wodalitsa fano; inde iwo asankha njira zaozao, ndipo moyo wao ukondwerera m'zonyansa zao; Inenso ndidzasankha zodzinyenga nazo, ndipo ndidzatengera mantha ao pa iwo; pakuti pamene ndinaitana, panalibe woyankha; pamene ndinalankhula, iwo sanamve konse; koma anachita choipa m'maso mwanga, ndi kusankha chimene ndisanakondwere nacho. Imvani mau a Yehova, inu amene munthunthumira ndi mau ake; abale anu amene akudani inu, amene anaponya inu kunja chifukwa cha dzina langa, iwo anati, Yehova alemekezedwe, kuti ife tione kusangalala kwanu; koma iwo adzakhala ndi manyazi. Mau a phokoso achokera m'mudzi, mau ochokera m'Kachisi, mau a Yehova amene abwezera adani ake chilango. Mkazi asanamve zowawa, anabala mwana; kupweteka kwake kusanadze, anabala mwana wamwamuna. Ndani anamva kanthu kotereko? Ndani anaona zinthu zoterezo? Kodi dziko lidzabadwa tsiku limodzi? Kodi mtundu udzabadwa modzidzimutsa? Pakuti pamene Ziyoni anamva zowawa, pomwepo anabala anake. Kodi Ine ndidzafikitsira mkazi nthawi yakutula osamtulitsa? Ati Yehova; kodi Ine amene ndibalitsa ndidzatseka mimba? Ati Mulungu wako. Sangalalani inu pamodzi ndi Yerusalemu, ndipo kondwani chifukwa cha iye, inu nonse amene mumkonda; sangalalani kokondwa pamodzi ndi iye, inu nonse akumlira maliro; kuti mukayamwe ndi kukhuta ndi mawere a zitonthozo zake; kuti mukafinye mkaka ndi kukondwerera ndi unyinji wa ulemerero wake. Pakuti atero Yehova, Taonani ndidzamfikitsira mtendere ngati mtsinje, ndi ulemerero wa amitundu ngati mtsinje wosefukira. Inu mudzayamwa, ndi kunyamulidwa pambali, ndi kululuzidwa pa maondo. Monga munthu amene amake amtonthoza mtima, momwemo ndidzatonthoza mtima wanu; ndipo mudzatonthozedwa mtima m'Yerusalemu. Ndipo mudzachiona, ndipo mtima wanu udzasangalala, ndipo mafupa anu adzakula ngati msipu; ndipo dzanja la Yehova lidzadziwika ndi atumiki ake, ndipo adzakwiyira adani ake. Pakuti taonani, Yehova adzafika m'moto, ndi magaleta ake adzafanana ndi kamvulumvulu; kubwezera mkwiyo wake ndi ukali, ndi kudzudzula ndi malawi amoto. Pakuti Yehova adzatsutsana ndi moto, ndi lupanga lake, ndi anthu onse; ndi ophedwa a Yehova adzakhala ambiri. Iwo amene adzipatulitsa nadziyeretsa, kuti amuke kuminda tsatanetsatane, ndi kudya nyama ya nkhumba, ndi chonyansa, ndi mbewa, adzathedwa pamodzi, ati Yehova. Pakuti Ine ndidziwa ntchito zao ndi maganizo ao; nthawi ikudza yakudzasonkhanitsa Ine a mitundu yonse ndi zinenedwe zonse, ndipo adzafika nadzaona ulemerero wanga. Ndipo ndidzaika chizindikiro pakati pao, ndipo ndidzatumiza onse amene apulumuka mwa iwo kwa amitundu, kwa Tarisisi, kwa Puti ndi kwa Aludi, okoka uta kwa Tubala ndi Yavani, kuzisumbu zakutali, amene sanamve mbiri yanga, ngakhale kuona ulemerero wanga; ndipo adzabukitsa ulemerero wanga pakati pa amitundu. Ndipo iwo adzatenga abale anu onse mwa amitundu onse akhale nsembe ya kwa Yehova; adzabwera nao pa akavalo, ndi m'magaleta, ndi m'machila, ndi pa nyuru, ndi pa ngamira, kudza kuphiri langa lopatulika ku Yerusalemu, ati Yehova, monga ana a Israele abwera nazo nsembe zao m'chotengera chokonzeka kunyumba ya Yehova. Ndipo ena a iwo ndidzawatenga akhale ansembe ndi Alevi, ati Yehova. Pakuti monga m'mwamba mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano limene ndidzalenga, lidzakhalabe pamaso pa Ine, ati Yehova, momwemo adzakhalabe ana anu ndi dzina lanu. Ndipo kudzakhala kuti kuyambira pa mwezi wokhala kufikira ku unzake, ndi kuyambira pa Sabata lina kufikira kulinzake, anthu onse adzafika kudzapembedzera pamaso pa Ine, ati Yehova. Ndipo iwo adzatuluka ndi kuyang'ana mitembo ya anthu amene andilakwira Ine, pakuti mphutsi yao sidzafa, pena moto wao sudzazimidwa; ndipo iwo adzanyansa anthu onse. Mau a Yeremiya mwana wa Hilikiya, wa ansembe amene anali ku Anatoti m'dziko la Benjamini; amene anamdzera mau a Yehova masiku a Yosiya mwana wake wa Amoni, mfumu ya Ayuda chaka chakhumi ndi chitatu cha ufumu wake. Anamdzeranso masiku a Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, kufikira Zedekiya mwana wake wa Yosiya mfumu ya Yuda atatsiriza zaka khumi ndi chimodzi; kufikira a ku Yerusalemu anatengedwa ndende mwezi wachisanu. Ndipo anadza kwa ine mau a Yehova, kuti, Ndisanakulenge iwe m'mimba ndinakudziwa, ndipo usanabadwe ndinakupatula iwe; ndinakuika kuti ukhale mneneri wa mitundu ya anthu. Ndipo ndinati, Ha, Ambuye Mulungu! Taonani, sindithai kunena pakuti ndili mwana. Koma Yehova anati kwa ine, Usati, ndine mwana pakuti udzanka kwa yense amene ndidzakutumako iwe, nudzanena chonse chimene ndidzakuuza. Usaope nkhope zao; chifukwa Ine ndili ndi iwe kuti ndikulanditse iwe, ati Yehova. Ndipo Yehova anatulutsa dzanja lake, nakhudza pakamwa panga; nati Yehova kwa ine, Taona ndaika mau anga m'kamwa mwako; penyatu, lero ndakuika ulamulire mitundu ya anthu ndi maufumu, kuti uzule, upasule, uononge, ugwetse, umange, ubzale. Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, kuti, Yeremiya, uona chiyani? Ndipo ndinati, Ine ndiona nthyole ya katungurume. Ndipo Yehova anati kwa ine, Waona bwino pakuti Ine ndidzadikira mau anga kuwachita. Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine nthawi yachiwiri, kuti, Uona chiyani? Ndipo ndinati, Ine ndiona mphika wogaduka; ndi pakamwa pake unafulatira kumpoto. Ndipo Yehova anati kwa ine, Kuchokera kumpoto choipa chidzatulukira onse okhala m'dziko. Pakuti taona, ndidzaitana mabanja onse a maufumu a kumpoto, ati Yehova; ndipo adzafika nadzaika yense mpando wachifumu wake pa zipata za Yerusalemu, ndi pa malinga onse ozinga pamenepo, ndi pa midzi yonse ya Yuda. Ndipo ndidzanena nao za maweruzo anga akuweruzira zoipa zao zonse; popeza anandisiya Ine, nafukizira milungu ina, nagwadira ntchito za manja ao. Koma iwe ukwinde m'chuuno mwako, nuuke, nunene kwa iwo zonse zimene ndikuuza iwe; usaope nkhope zao ndingakuopetse iwe pamaso pao. Chifukwa, taona, ndakuyesa iwe lero mudzi walinga, mzati wachitsulo, makoma amkuwa, pa dziko lonse, ndi pa mafumu a Yuda, ndi pa akulu ake, ndi pa ansembe ake, ndi pa anthu a m'dziko. Ndipo adzamenyana ndi iwe; koma sadzakuposa; chifukwa Ine ndili ndi iwe, ati Yehova, kukulanditsa. Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, nati, Pita nufuule m'makutu a Yerusalemu, kuti, Yehova atero, Ndikumbukira za iwe kukoma mtima kwa ubwana wako, chikondi cha matomedwe ako; muja unanditsata m'chipululu m'dziko losabzalamo. Israele anali wopatulikira Yehova, zipatso zoundukula za zopindula zake; onse amene adzamudya iye adzayesedwa opalamula; choipa chidzawagwera, ati Yehova. Tamvani mau a Yehova, iwe nyumba ya Yakobo, ndi inu mabanja onse a nyumba ya Israele; atero Yehova, Atate anu apeza chosalungama chanji mwa Ine, kuti andichokera kunka kutali, natsata zachabe, nasanduka achabe? Osati Ali kuti Yehova amene anatikweza kuchokera kudziko la Ejipito, natitsogolera m'chipululu, m'dziko loti see ndi la maenje, m'dziko la chilala ndi la mthunzi wa imfa, m'dziko losapitanso anthu, losamangamo anthu? Ndipo ndinakulowetsani m'dziko la minda, kuti mudye zipatso zake, ndi zabwino zake; koma pamene munalowa, munaipitsa dziko langa, ndi kuyesa cholandira changa chonyansa. Ansembe sanati, Ali kuti Yehova? Ndi iwo amene agwira malamulo sandidziwa Ine; ndi abusa omwe anandilakwira Ine, ndi aneneri ananenera mwa Baala, natsata zinthu zosapindula. Chifukwa chake ndidzatsutsananso nanu, ati Yehova, ndi ana a ana anu ndidzatsutsana nao. Pakuti pitani ku zisumbu za Kitimu nimuone; tumizani ku Kedara nimulingalire bwino; nimuone ngati chinalipo chotere. Kodi mtundu wa anthu unasintha milungu yao, imene siili milungu? Koma anthu anga anasintha ulemerero wao ndi chosapindula. Muzizwe pamenepo, miyamba inu, muope kwambiri, mukhale ouma, ati Yehova. Pakuti anthu anga anachita zoipa ziwiri; anandisiya Ine kasupe wa madzi amoyo, nadziboolera zitsime, zitsime zong'aluka, zosakhalamo madzi. Kodi Israele ndi mtumiki? Kodi ndiye kapolo wobadwa m'nyumba? Afunkhidwa bwanji? Ana a mikango anambangulira iye, nakweza mau; anapasula dziko lake, midzi yake yatenthedwa, mulibenso wokhalamo. Ananso a Nofi ndi a Tapanesi, anaswa pakati pamtu pako. Kodi sunadzichitira ichi iwe wekha popeza unasiya Yehova Mulungu wako, pamene anatsogolera iwe panjira? Tsopano uli nacho chiyani m'njira ya ku Ejipito, kumwa madzi a Sihori? Uli nacho chiyani m'njira ya ku Asiriya, kumwa madzi a m'mtsinje? Choipa chako dzidzakulanga iwe, mabwerero ako adzakudzudzula iwe; dziwa, nuone, kuti ichi ndi choipa ndi chowawa, kuti wasiya Yehova Mulungu wako, ndi kuti kundiopa Ine sikuli mwa iwe, ati Yehova Mulungu wa makamu. Pakuti kale lomwe ndinathyola goli lako, ndi kudula zomangira zako; ndipo unati, Sindidzakutumikirani, pakuti pa zitunda zonse zazitali, ndi patsinde pa mitengo yonse yaiwisi unawerama, ndi kuchita dama. Ndipo Ine ndinakuoka mpesa wangwiro, mbeu yoona; kodi bwanji wandisandukira Ine mbeu yopanda pake, ya mpesa wachilendo? Pakuti ngakhale usamba ndi soda, ndi kudzitengera sopo wambiri, mphulupulu zako zidziwika pamaso panga, ati Yehova Mulungu. Bwanji uti, Sindinaipitsidwa, sindinatsata Abaala? Ona njira yako m'chigwa, dziwa chimene wachichita; ndiwe ngamira yothamanga yoyenda m'njira zake; mbidzi yozolowera m'chipululu, yopumira mphepo pakufuna pake; pokomana nayo ndani adzaibweza? Onse amene aifuna sadzadzilemetsa; adzaipeza m'mwezi wake. Kaniza phazi lako lisakhale losavala nsapato, ndi m'mero mwako musakhale ndi ludzu; koma unati, Palibe chiyembekezo, iai; pakuti ndakonda alendo, ndipo ndidzatsata pambuyo pao. Monga mbala ili ndi manyazi pamene igwidwa, chomwecho nyumba ya Israele ili ndi manyazi; iwo, mafumu ao, akulu ao, ansembe ao, ndi aneneri ao; amene ati kwa mtengo, Iwe ndiwe atate wanga; ndi kwa mwala, Wandibala; pakuti anandipatsa Ine mbuyo, si nkhope yao; koma m'nthawi ya kuvutidwa kwao adzati, Ukani, tipulumutseni. Koma ili kuti milungu yako imene wadzipangira? Iuke, ikupulumutse iwe m'nthawi ya kuvutidwa kwako; pakuti milungu yako ilingana ndi kuchuluka kwa midzi yako, Yuda iwe. Chifukwa chanji mudzatsutsana ndi Ine nonse? Mwandilakwira Ine, ati Yehova. Ndapanda ana anu mwachabe; sanamvere kulanga; lupanga lanu ladya aneneri anu, monga mkango wakuononga. Mbadwo inu, taonani mau a Yehova. Kodi ndakhala kwa Israele chipululu? Kapena dziko la mdima woti bii? Chifukwa ninji ati anthu anga, Tamasuka sitidzabweranso konse kwa Inu? Kodi angathe namwali kuiwala zokometsera zake, kapena mkwitibwi zovala zake? Koma anthu anga andiiwala Ine masiku osawerengeka. Kodi sukonzadi njira yako kufunafuna chilakolako? Chifukwa chake waphunzitsa akazi oipa njira zako. Ndiponso m'nsalu zako wapezeka mwazi wa miyoyo ya aumphawi osachimwa; sunawapeza pakuboola, koma ponsepo. Koma unati, Ndili wosachimwa ndithu; mkwiyo wake wachoka pa ine. Taona, ndidzakuweruza iwe, chifukwa uti, Sindinachimwa. Bwanji uyendayenda kwambiri ndi kusintha njira yako? Udzachitanso manyazi ndi Ejipito monga unachita manyazi ndi Asiriya. Koma udzatuluka kwa iyenso, manja ako pamtu pako; pakuti Yehova wakana zokhulupirira zako, ndipo sudzapindula m'menemo. Amati, Ngati mwamuna achotsa mkazi wake, ndipo amchokera iye, nakhala mkazi wa wina, kodi adzabweranso kwa mkaziyo? Dzikolo kodi silidzaipitsidwa? Koma iwe wachita dama ndi mabwenzi ambiri; koma bweranso kwa Ine, ati Yehova. Kwezera maso ako kumapiri oti see, nuone: sanagona ndi iwe kuti? Panjira wakhalira iwo, monga Mwarabu m'chipululu; ndipo waipitsa dziko ndi zigololo zako, ndi zoipa zako. Ndipo mvula yakanidwa, ndipo panalibe mvula ya masika; ndipo unali ndi nkhope ya mkazi wadama, unakana manyazi. Kodi kuyambira tsopano sudzafuulira kwa Ine, Atate wanga, wotsogolera ubwana wanga ndinu? Kodi adzasunga mkwiyo wake kunthawi zonse? Kodi adzakudikira mpaka chimaliziro? Taona, wanena ndi kuchita zoipa monga unatero. Ndipo Yehova anati kwa ine masiku a Yosiya mfumu, Kodi waona chimene wachichita Israele, wobwerera m'mbuyo? Wakwera pa mapiri atali onse, ndi patsinde pa mitengo yaiwisi yonse, ndi kuchita dama pamenepo. Ndipo ndinati atachita zimenezo zonse, Adzabwera kwa Ine; koma sanabwere, ndipo mphwake wonyenga, Yuda, anaona. Ndipo ndinaona, kuti, ndingakhale ndikamchotsa Israele wobwerera m'mbuyo, ndi kumpatsa kalata wachilekaniro chifukwa cha kuchita chigololo iye, mphwake Yuda wonyenga sanaope, koma iye yemwe ananka nachita dama. Ndipo kunali kuti mbiri ya dama lake inaipitsa dziko, ndipo anachita chigololo ndi miyala ndi mitengo. Ndipo zingakhale zonsezi Yuda mphwake wonyenga sanabwere kwa Ine ndi mtima wake wonse, koma monama, ati Yehova. Ndipo Yehova anati kwa ine, Israele wobwerera anadzionetsa wolungama kopambana ndi Yuda wonyenga. Pita; nulalikire mau awa kuyang'ana kumpoto, ndi kuti, Bwera iwe Israele wobwerera, ati Yehova; sindidzakuyang'anira iwe ndi kukwiya; pakuti Ine ndili wachifundo, ati Yehova, sindidzakhala nako kukwiya kunthawi zonse. Koma vomereza zoipa zako, kuti walakwira Yehova Mulungu wako, ndi kupatukira mwa alendo patsinde pa mitengo yaiwisi yonse, ndipo sunamvera mau anga, ati Yehova. Bwerani, ananu obwerera, ati Yehova; pakuti Ine ndine mbuye wanu; ndipo ndidzakutengani inu mmodzimmodzi wa pa mudzi uliwonse, ndi awiriawiri a pa banja lililonse, ndi kukutengerani ku Ziyoni; ndipo ndidzakupatsani inu abusa monga mwa mtima wanga, adzakudyetsani inu nzeru ndi luntha. Ndipo padzaoneka, pamene mudzakhala ambiri ndi kuchuluka m'dzikomo masiku awo, ati Yehova, sadzatinso konse, Likasa la chipangano cha Yehova; silidzalowa m'mtima; sadzalikumbukira; sadzanka kukaliona, sadzachitanso konse. Pa nthawi yomweyo adzatcha Yerusalemu mpando wa Yehova; ndipo mitundu yonse idzasonkhanidwa kumeneko, ku dzina la Yehova, ku Yerusalemu; ndipo sadzayendanso konse m'kuumirira kwa mtima wao woipa. Masiku omwewo nyumba ya Yuda idzayenderena ndi nyumba ya Israele, ndipo adzatuluka pamodzi kudziko la kumpoto kunka ku dziko limene ndinapatsa makolo anu kuti alowemo. Koma Ine ndinati, Ndidzakuika iwe bwanji mwa ana, ndi kupatsa iwe dziko lokondweretsa, cholowa chabwino cha makamu a mitundu ya anthu? Ndipo ndinati mudzanditcha Ine, Atate wanga; osatembenuka kuleka kunditsata Ine. Ndithu monga mkazi achokera mwamuna wake monyenga, chomwecho mwachita ndi Ine monyenga, inu nyumba ya Israele, ati Yehova. Mau amveka pa mapiri oti see, kulira ndi kupempha kwa ana a Israele; pakuti anaipitsa njira yao, naiwala Yehova Mulungu wao. Bwerani, ana inu obwerera, ndidzachiritsa mabwerero anu. Taonani, tadza kwa Inu; pakuti ndinu Yehova Mulungu wathu. Ndithu akhulupirira mwachabe chithandizo cha kuzitunda, ndi phokoso la kumapiri; ndithu mwa Yehova Mulungu wathu muli chipulumutso cha Israele. Ndipo chochititsa manyazi chinathetsa ntchito za atate athu kuyambira ubwana wathu; nkhosa zao ndi zoweta zao, ana ao aamuna ndi aakazi. Tigone m'manyazi athu, kunyala kwathu kutifunde ife; pakuti tamchimwira Yehova Mulungu wathu, ife ndi makolo athu, kuyambira ubwana wathu kufikira lero lomwe; ndipo sitidamvera mau a Yehova Mulungu wathu. Ngati udzabwera, Israele, ati Yehova, udzabwera kwa Ine; ndipo ngati udzachotsa zonyansa zako pamaso panga sudzachotsedwa. Ndipo udzalumbira, Pali Yehova m'zoonadi, m'chiweruziro, ndi m'chilungamo; ndipo mitundu ya anthu idzadzidalitsa mwa Iye, ndipo mwa Iye adzatamandira. Pakuti Yehova atero kwa anthu a Yuda ndi kwa Yerusalemu, Limani masala anu, musabzale paminga. Mudzidulire nokha kwa Yehova, chotsani khungu la mitima yanu, amuna inu a Yuda ndi okhala m'Yerusalemu; ukali wanga ungatuluke ngati moto, ungatenthe kuti sangathe kuuzima, chifukwa cha kuipa kwa machitidwe anu. Nenani m'Yuda, lalikirani m'Yerusalemu, ndi kuti, Ombani lipenga m'dzikomo; fuulani, ndi kuti, Sonkhanani pamodzi, tilowe m'midzi ya malinga. Kwezani mbendera kuyang'ana ku Ziyoni; thawani kuti mupulumuke, musakhale; pakuti ndidza ndi choipa chochokera kumpoto ndi kuononga kwakukulu. Mkango wakwera kutuluka m'nkhalango mwake, ndipo woononga amitundu ali panjira, watuluka m'mbuto mwake kuti achititse dziko lako bwinja, kuti midzi yako ipasuke mulibenso wokhalamo. Pamenepo, valani chiguduli, lirani ndi kubuula; pakuti mkwiyo wa kuopsa wa Yehova sunabwerera pa ife. Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova, kuti mtima wa mfumu udzataika, ndi mitima ya akulu; ndipo ansembe adzazizwa, ndi aneneri adzadabwa. Ndipo ndinati, Ha, Yehova Mulungu! Ndithu mwanyenga kwambiri anthu awa ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mudzalandira mtendere; koma lupanga lafikira pamoyo. Pa nthawi yomweyo adzati kwa anthu awa ndi kwa Yerusalemu, Mphepo yotentha yochokera kumapiri oti see m'chipululu yopita kwa mwana wamkazi wa anthu anga, yosapetera, yosayeretsa; mphepo yolimba yochokera kumeneko idzandifika ine; tsopanonso ndidzaweruza iwo maweruzo. Taonani, adzadza ngati mitambo, ndi magaleta ake ngati kamvulumvulu; akavalo ake athamanga kopambana mphungu. Tsoka ife! Pakuti tapasuka. Iwe Yerusalemu, utsuke mtima wako kuchotsa zoipa kuti upulumuke. Maganizo ako achabe agona mwako masiku angati? Pakuti mau anena m'Dani nalalikira nsautso m'phiri la Efuremu: Mukumbutse mitundu ya anthu; taonani, lalikirani Yerusalemu, kuti owazinga ndi nkhondo afumira kudziko lakutali, nainenera midzi ya Yuda mau ao. Monga adindo a m'munda amzinga iye; chifukwa andipandukira Ine, ati Yehova. Njira yako ndi ntchito zako zinakuchitira izi; ichi ndicho choipa chako ndithu; chili chowawa ndithu, chifikira kumtima wako. Matumbo anga, matumbo anga! Ndipoteka pamtima panga penipeni; mtima wanga sukhala pansi m'kati mwanga; sindithai kutonthola; pakuti wamva, moyo wanga, mau a lipenga, mbiri ya nkhondo. Alalikira chipasuko chilalikire; pakuti dziko lonse lafunkhidwa; mahema anga afunkhidwa dzidzidzi, ndi nsalu zanga zotchinga m'kamphindi. Kufikira liti ndidzaona mbendera, ndi kumva kulira kwa lipenga? Pakuti anthu anga apusa, sandidziwa Ine; ali ana opulukira sazindikira; ali ochenjera kuchita choipa koma kuchita chabwino sakudziwa. Ndinaona dziko lapansi, ndipo taona, linali lopasuka lopanda kanthu; ndipo ndinaona kumwamba, kunalibe kuunika. Ndinaona mapiri, taona ananthunthumira; ndipo zitunda zonse zinagwedezeka. Ndinaona, ndipo taona, panalibe munthu, ndi mbalame zonse zakumwamba zinathawa. Ndinaona, ndipo taona, munda wazipatso unali chipululu, ndipo midzi yake yonse inapasuka pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa mkwiyo wake woopsa. Pakuti Yehova atero, Dziko lonse lidzakhala bwinja koma sindidzatsirizitsa. Chifukwa chimenecho dziko lidzalira maliro, ndipo kumwamba kudzada; chifukwa ndanena, ndatsimikiza mtima, sindinatembenuka, sindidzabwerera pamenepo. Mudzi wonse uthawa m'phokoso la apakavalo ndi amauta; adzalowa m'nkhalango, adzakwera pamiyala; midzi yonse idzasiyidwa, ndipo simudzakhala munthu m'menemo. Nanga iwe, udzachita chiyani pamene udzafunkhidwa? Ngakhale udziveka ndi zofiira, ngakhale udziveka ndi zokometsera zagolide, ngakhale udzikuzira maso ako ndi kupaka, udzikometsera pachabe; mabwenzi adzakunyoza adzafuna moyo wako. Pakuti ndamva kubuula ngati kwa mkazi wobala, ndi msauko ngati wa mkazi wobala mwana wake woyamba, mau a mwana wamkazi wa Ziyoni wakupuma mosiyiza, wakutambasula manja ake, ndi kuti, Tsoka ine tsopano! Pakuti moyo wanga walefuka chifukwa cha ambanda. Thamangani inu kwina ndi kwina m'miseu ya Yerusalemu, taonanitu, dziwani, ndi kufunafuna m'mabwalo ake, kapena mukapeza munthu, kapena alipo wakuchita zolungama, wakufuna choonadi; ndipo ndidzamkhululukira. Ndipo ngakhale ati, Pali Yehova; komatu alumbira monama. Yehova Inu, maso anu sali pachoonadi kodi? Munawapanda iwo, koma sanaphwetekedwe mtima; munawatha iwo, koma akana kudzudzulidwa; alimbitsa nkhope zao koposa mwala; akana kubwera. Ndipo ine ndinati, Ndithu amenewo ali aumphawi; ali opusa; pakuti sadziwa njira ya Yehova, kapena chiweruzo cha Mulungu wao. Ine ndidzanka kwa akulu, ndidzanena ndi iwo; pakuti adziwa njira ya Yehova, ndi chiweruzo cha Mulungu wao. Koma awa anavomerezana nathyola goli, nadula zomangira zao. Chifukwa chake mkango wotuluka m'nkhalango udzawapha, ndi mmbulu wa madzulo udzawafunkha, nyalugwe adzakhalira m'midzi mwao, onse amene atulukamo adzamwetulidwa; pakuti zolakwa zili zambiri, ndi mabwerero ao achuluka. Bwanji ndidzakhululukira iwe? Pamenepo ana ako andisiya Ine, nalumbira pa iyo yosati milungu; pamene ndinakhutitsa iwo, anachita chigololo, nasonkhana masonkhano m'nyumba za adama. Anali onga akavalo okhuta mamawa; yense wakumemesera mkazi wa mnansi wake. Kodi sindidzawalanga chifukwa cha zimenezi? Ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera chilango mtundu woterewu? Kwerani pa makoma ake nimupasule; koma musatsirize konse; chotsani nthambi zake pakuti sizili za Yehova. Pakuti nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda zinandichitira monyenga kwambiri, ati Yehova. Akana Yehova, ndi kuti, Si ndiye; choipa sichidzatifika ife; sitidzaona kapena lupanga kapena njala; ndipo aneneri adzasanduka mphepo, ndipo mwa iwo mulibe mau; chomwecho chidzachitidwa ndi iwo. Chifukwa chake Yehova Mulungu wa makamu atero, Chifukwa munena mau awa, taona, ndidzayesa mau anga akhale m'kamwa mwako ngati moto, anthu awa ndidzayesa nkhuni, ndipo udzawatha iwo. Taonani, ndidzatengera pa inu mtundu wa anthu akutali, inu nyumba ya Israele, ati Yehova; ndi mtundu wolimba, ndi mtundu wakalekale, mtundu umene chinenero chake simudziwa, ngakhale kumva zonena zao. Phodo lao lili ngati manda apululu, onsewo ndiwo olimba. Adzadya zokolola zako, ndi mkate wako, umene ana ako aamuna ndi aakazi ayenera kudya; adzadya nkhosa zako ndi zoweta zako; adzadya mphesa zako ndi nkhuyu zako; adzapasula ndi lupanga midzi yamalinga yako, imene ukhulupiriramo. Koma masiku onsewo, ati Yehova, sindidzatsirizitsa konse ndi iwe. Ndipo padzakhala pamene mudzati, Chifukwa chanji Yehova Mulungu wathu atichitira ife zonse izi? Ndipo udzayankha kwa iwo, Monga ngati mwandisiya Ine, ndi kutumikira milungu yachilendo m'dziko lanu, momwemo mudzatumikira alendo m'dziko silili lanu. Nenani ichi m'nyumba ya Yakobo, lalikirani m'Yuda, kuti, Tamvanitu ichi, inu anthu opusa, ndi opanda nzeru; ali ndi maso koma osaona, ali ndi makutu koma osamva; Kodi simundiopa Ine? Ati Yehova: simudzanthunthumira pamaso pa Ine, amene ndinaika mchenga chilekaniro cha nyanja, ndi lemba lamuyaya kuti isapitirirepo? Ndipo ngakhale mafunde ake achita gavigavi, alephera; ngakhale akokoma, sangathe kupitirirapo. Koma anthu awa ali ndi mtima woukirana ndi wopikisana; anapanduka nachoka. Ndipo sanena m'mtima mwao, Tiopetu Yehova Mulungu wathu wopatsa mvula yoyamba ndi yamasika, m'nyengo yake; atisungira ife masabata olamulidwa a masika. Mphulupulu zanu zachotsa zimenezi, ndi zochimwa zanu zakukanitsani inu zinthu zabwino. Pakuti mwa anthu anga aoneka anthu oipa; adikira monga akucha misampha; acha khwekhwe, agwira anthu. Monga chikwere chodzala ndi mbalame, chomwecho nyumba zao zadzala ndi chinyengo; chifukwa chake akula, alemera. Anenepa, anyezimira; inde apitiriza kuchita zoipa; sanenera ana amasiye mlandu wao, kuti apindule; mlandu wa aumphawi saweruza. Sindidzawalanga kodi chifukwa cha zimenezi? Ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera chilango mtundu wotere? Chodabwitsa ndi choopsa chaoneka m'dzikomo; aneneri anenera monyenga nathandiza ansembe pakulamulira kwao; ndipo anthu anga akonda zotere; ndipo mudzachita chiyani pomalizira pake? Ananu a Benjamini, pulumukani pothawa pakati pa Yerusalemu, ombani lipenga m'Tekowa, kwezani chizindikiro m'Betehakeremu; pakuti chaoneka choipa chotuluka m'mpoto ndi kuononga kwakukulu. Ndidzachotsa mwana wamkazi wa Ziyoni mkazi wokoma ndi wololopoka. Abusa ndi nkhosa zao adzadza kwa iye; adzamanga mahema ao pomzinga iye; adzadya yense pokhala pake. Lalikirani nkhondo yakumenyana ndi iye; ukani, tikwere pakati pa usana. Tsoka kwa ife! Pakuti dzuwa lapendeka, mithunzi ya madzulo yatambasuka. Ukani, tiyende usiku, tipasule nyumba zake. Pakuti Yehova wa makamu atero, Dulani mitengo, unjikani nthumbira pomenyana ndi Yerusalemu; mudzi wakudzalangidwa ndi uwu; m'kati mwake modzala nsautso. Monga kasupe atulutsa madzi ake, chomwecho atulutsa zoipa zake; chiwawa ndi kufunkha zimveka m'kati mwake; pamaso panga masiku onse pali kulira ndi mabala. Ulangizidwe, Yerusalemu, ungakuchokere moyo wanga, ndingakuyese iwe bwinja, dziko losakhalamo anthu. Yehova wa makamu atero, Adzakunkha otsalira a Israele monga mpesa; bweza dzanja lako monga wakutchera mphesa m'madengu ake. Ndidzanena ndi yani, ndidzachita mboni kwa yani, kuti amve? Taona khutu lao lili losadulidwa, ndipo sangathe kumva; taona, mau a Yehova awatonzetsa iwo; sakondwera nao. Chifukwa chake ndadzala ndi ukali wa Yehova; ndalema ndi kudzikaniza; tsanulirani pa ana a pabwalo, ndi pa masonkhano a anyamata, pakuti ngakhale mwamuna ndi mkazi wake adzatengedwa, okalamba ndi iye amene achuluka masiku ake. Nyumba zao zidzasanduka za ena, pamodzi ndi minda yao ndi akazi ao; pakuti ndidzatambasula dzanja langa pa okhala m'dziko, ati Yehova. Pakuti kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu onse akhala akusirira; ndiponso kuyambira mneneri kufikira wansembe onse achita monyenga. Ndiponso apoletsa bala la anthu anga pang'onong'ono, ndi kuti, Mtendere, mtendere; koma palibe mtendere. Kodi anakhala ndi manyazi pamene anachita chonyansa? Iai, sanakhale konse ndi manyazi, sanathe kunyala; chifukwa chake adzagwa mwa iwo akugwa; panthawi pamene ndidzafika kwa iwo, adzagwetsedwa, ati Yehova. Yehova atero, Imani m'njira ndi kuona, funsani za mayendedwe akale, m'menemo muli njira yabwino, muyende m'menemo, ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu; koma anati, Sitidzayendamo. Ndipo ndinaika alonda oyang'anira inu, ndi kuti, Mverani mau a lipenga; koma anati, Sitidzamvera. Chifukwa chake tamverani, amitundu inu, dziwani, msonkhano inu, chimene chili mwa iwo. Tamva, dziko lapansi iwe; taona, Ine ndidzatengera choipa pa anthu awa, chipatso cha maganizo ao, pakuti sanamvere mau anga, kapena chilamulo changa, koma wachikana. Lubani andifumiranji ku Sheba, ndi nzimbe ku dziko lakutali? Nsembe zopsereza zanu sizindisekeretsa, nsembe zophera zanu sizindikondweretsa Ine. Chifukwa chake atero Yehova, Taona, ndidzaikira anthuwa zophunthwitsa; ndipo atate ndi ana adzakhumudwa nazo pamodzi; munthu ndi mnzake adzatayika. Yehova atero, Taona, mtundu wa anthu uchokera kumpoto; ndi mtundu waukulu adzaukitsidwa ku malekezero a dziko lapansi. Agwira uta ndi nthungo; ali ankharwe, alibe chifundo; mau ao aphokosera ngati nyanja, akwera pa akavalo; aguba monga anthu ofuna kumenyana nkhondo ndi iwe, mwana wamkazi wa Ziyoni. Tamva ife mbiri yake; manja athu alefuka, yatigwira nkhawa ndi zowawa ngati za mkazi wobala. Usatulukire kumunda, usayenda m'njira; pakuti lupanga la amaliwongo ndi mantha ali m'mbali zonse. Iwe mwana wamkazi wa anthu anga, udziveke ndi chiguduli, ndi kuvimvinika m'phulusa; ulire maliro ngati a mwana wamwamuna wa yekha, kulira kowawa koposa; pakuti wakufunkha adzatifikira ife motidzidzimutsa. Ndakuyesa iwe nsanja ndi linga mwa anthu anga, kuti udziwe ndi kuyesa njira yao. Onse ali opikisana ndithu, ayendayenda ndi maugogodi; ndiwo mkuwa ndi chitsulo; onsewa achita movunda; mvukuto yatenthedwa ndi moto; mtovu watha ndi moto wa ng'anjo; ayenga chabe; pakuti oipa sachotsedwa. Anthu adzawatcha nthale ya siliva, pakuti Yehova wakana iwo. Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, kuti, Ima m'chipata cha nyumba ya Yehova, lalikira m'menemo mau awa, ndi kuti, Tamvani mau a Yehova, inu nonse a Yuda, amene alowa m'zipata izi kuti mugwadire Yehova. Yehova wa makamu atero, Mulungu wa Israele, Konzani njira zanu ndi machitidwe anu, ndipo ndidzakukhalitsani inu m'malo ano. Musakhulupirire mau onama, kuti, Kachisi wa Yehova, Kachisi wa Yehova, Kachisi wa Yehova ndi awa. Pakuti mukakonzatu njira zanu ndi machitidwe anu; ndi kuweruzatu milandu ya munthu ndi mnansi wake; ndi kuleka kutsendereza mlendo, ndi wamasiye, ndi mkazi wamasiye, osakhetsa mwazi wosachimwa m'malo muno, osatsata milungu ina ndi kudziipitsa nayo; ndipo ndidzakukhazikani inu m'malo muno, m'dziko limene ndinapatsa makolo anu, kuyambira kale lomwe kufikira muyaya. Taonani, mukhulupirira mau onama, osapindulitsa. Kodi mudzapha, ndi kuba, ndi kuchita chigololo, ndi kulumbira zonama, ndi kupereka nsembe kwa Baala, ndi kutsata milungu ina imene simunaidziwa, ndi kudza ndi kuima pamaso panga m'nyumba yino, imene itchedwa dzina langa, ndi kuti, Talanditsidwa; kuti muchite zonyansa izi? Kodi nyumba yino, imene itchedwa dzina langa, ikhala phanga la okwatula pamaso panu? Taona, Ine ndachiona, ati Yehova. Koma pitani tsopano kumalo anga amene anali m'Silo, m'mene ndinaikamo dzina langa poyamba paja, ndi kuona chimene ndinachitira chifukwa cha zoipa za anthu anga Israele. Ndipo tsopano, chifukwa munachita ntchito zonsezi, ati Yehova, ndipo ndinanena kwa inu, ndi kuuka mamawa ndi kunena, koma simunamva; ndipo ndinakuitanani inu, koma simunayankha; chifukwa chake ndidzaichitira nyumba iyi, imene itchedwa dzina langa, imene mukhulupirirayi, ndipo ndidzachitira malo amene ndinakupatsani inu ndi makolo anu, monga ndinachitira Silo. Ndipo ndidzakuchotsani inu pamaso panga, monga ndinachotsa abale anu onse, mbeu zonse za Efuremu. Chifukwa chake iwe usapempherere anthu awa, usawakwezere iwo mfuu kapena pemphero, usandipembedze; pakuti Ine sindidzakumvera iwe. Kodi suona iwe chimene achichita m'midzi ya Yuda ndi m'miseu ya Yerusalemu? Ana atola nkhuni, atate akoleza moto, akazi akanyanga ufa, kuti aumbe mikate ya mfumu yaikazi ya kumwamba, athirire milungu ina nsembe yothira, kuti autse mkwiyo wanga. Kodi autsa mkwiyo wanga? Ati Yehova; kodi sadziutsira okha manyazi a nkhope zao? Chifukwa chake, ati Ambuye Mulungu, Taonani, mkwiyo wanga ndi ukali wanga udzathiridwa pa malo ano, pa anthu, ndi pa nyama, ndi pa mitengo ya m'munda, ndi pa zipatso zapansi; ndipo udzatentha osazima. Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele; Ikani zopereka zopsereza zanu pa nsembe zophera zanu, nimudye nyama. Pakuti sindinanena kwa makolo anu, tsiku lija ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito, ngakhale kuwauza nsembe zopsereza kapena zophera; koma chinthu ichi ndinawauza, kuti, Mverani mau anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu, ndipo inu mudzakhala anthu anga; nimuyende m'njira yonse imene ndakuuzani inu, kuti chikukomereni. Koma sanamvere, sanatchere khutu, koma anayenda m'upo ndi m'kuuma kwa mtima wao woipa, nabwerera chambuyo osayenda m'tsogolo. Chiyambire tsiku limene makolo anu anatuluka m'dziko la Ejipito kufikira lero lino, ndatumiza kwa inu atumiki anga onse, aneneri, tsiku ndi tsiku, kuuka mamawa ndi kuwatumiza iwo; koma sanandimvere Ine sanatchera khutu lao, koma anaumitsa khosi lao; anaipa koposa makolo ao. Ndipo uzinena kwa iwo mau awa onse, koma sadzakumvera iwe; ndipo udzawaitananso; koma sadzakuyankha iwe. Ndipo udzati kwa iwo, Umene ndi mtundu wosamvera mau a Yehova Mulungu wao, wosalola kulangizidwa, choonadi chatha, chadulidwa pakamwa pao. Meta tsitsi lako, iwe Yerusalemu, nulitaye, nukweze maliro pa mapiri oti see; pakuti Yehova wakana ndi kusiya mbadwo umene aukwiyira. Pakuti ana a Yuda anachita choipa pamaso panga, ati Yehova; naika zonyansa zao m'nyumba yotchedwa dzina langa, kuti alipitse. Namanga akachisi a ku Tofeti, kuli m'chigwa cha mwana wa Hinomu, kuti atenthe m'moto ana ao aamuna ndi aakazi; chimene sindinauza iwo, sichinalowa m'mtima mwanga. Chifukwa chake, taonani, masiku alikudza, ati Yehova, ndipo sadzatchedwanso Tofeti, kapena Chigwa cha mwana wa Hinomu, koma Chigwa cha Kuphera; pakuti adzataya m'Tofeti, kufikira malo akuikamo adzasowa. Ndipo mitembo ya anthu awa idzakhala zakudya za mbalame za mlengalenga, ndi za zilombo za dziko lapansi; palibe amene adzaziopsa. Ndipo ndidzaletsa m'midzi ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, mau akukondwa ndi mau akusekera, ndi mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi; pakuti dziko lidzasanduka bwinja. Nthawi yomweyo, ati Yehova, adzatulutsa m'manda mwao mafupa a mafumu a Yuda, ndi mafupa a akulu ake, ndi mafupa a ansembe, ndi mafupa a aneneri, ndi mafupa a okhala m'Yerusalemu, ndipo udzawayanika padzuwa, ndi pamwezi, ndi pa khamu lonse la kuthambo, limene analikonda, ndi kulitumikira, ndi kulitsata, ndi kulifuna, ndi kuligwadira; sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ndowe panthaka. Ndipo otsala onse amene akutsala pa banja loipa ili adzasankha imfa koposa moyo, ndiwo amene atsala m'malo monse m'mene ndinawaingiramo, ati Yehova wa makamu. Ndiponso udzati kwa iwo, Atero Yehova, Kodi adzagwa, osaukanso? Kodi wina adzachoka, osabweranso? Bwanji abwerera anthu awa a Yerusalemu chibwererere? Agwiritsa chinyengo, akana kubwera. Ndinatchera khutu, ndinamva koma sananene bwino; panalibe munthu amene anatembenuka kusiya zoipa zake, ndi kuti, Ndachita chiyani? Yense anatembenukira njira yake, monga akavalo athamangira m'nkhondo. Inde, chumba cha mlengalenga chidziwa nyengo zake; ndipo njiwa ndi namzeze ndi chingalu ziyang'anira nyengo yakufika kwao; koma anthu anga sadziwa chiweruziro cha Yehova. Bwanji muti, Tili ndi nzeru ife, ndi malamulo a Yehova ali ndi ife? Koma, taona, peni lonyenga la alembi lachita zonyenga. Anzeru ali ndi manyazi, athedwa nzeru nagwidwa; taonani, akana mau a Yehova; ali nayo nzeru yotani? Chifukwa chake ndidzapereka akazi ao kwa ena, ndi minda yao kwa iwo adzalowamo; pakuti onse kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu asirirasirira; kuyambira mneneri kufikira wansembe onse achita zonyenga. Ndipo analipoletsa pang'ono bala la mwana wamkazi wa anthu anga, ndi kuti, Mtendere, mtendere; posakhala mtendere. Kodi anakhala ndi manyazi pamene anachita zonyansa? Iai, sanakhale ndi manyazi, sananyale; chifukwa chake adzagwa mwa iwo amene akugwa, nthawi ya kuyang'aniridwa kwao adzagwetsedwa, ati Yehova. Kuwatha ndidzawathetsa iwo, ati Yehova, sipadzakhala mphesa pampesa, kapena nkhuyu pamkuyu, ndipo tsamba lidzafota, ndipo zinthu ndinawapatsa zidzawachokera. Tikhaliranji ife? Tasonkhanani, tilowe m'midzi yamalinga, tikhale chete m'menemo; pakuti Yehova Mulungu wathu watikhalitsa ife chete, natipatsa ife madzi a ndulu timwe, pakuti tamchimwira Yehova. Tinayang'anira mtendere, koma panalibe zabwino; ndi nthawi ya moyo, ndipo taona kuopsedwa! Kumina kwa akavalo ake kunamveka ku Dani; dziko lonse linanthunthumira pa kulira kwa akavalo akewo olimba; chifukwa afika, nadya dziko ndi zonse za momwemo; mudzi ndi amene akhalamo. Pakuti, taonani, ndidzatumiza pa inu njoka, mphiri, zosalola kuitanidwa; ndipo zidzakulumani inu, ati Yehova. Ha, ndikadatonthoza mtima wanga kuletsa chisoni chake? Mtima wanga walefuka m'kati mwa ine. Taonani, mau a kulira kwa mwana wamkazi wa anthu anga ochokera kudziko lakutali: Kodi m'Ziyoni mulibe Yehova? Kodi mulibe mfumu yake? Chifukwa chanji andiputa Ine ndi mafano ao osema, ndi zachabe zachilendo? Masika apita, mphakasa yatha, ndipo ife sitinapulumutsidwe. Bala la mwana wamkazi wa anthu anga ndaphwetekwa nalo; ndada mtima; kudabwa kwandigwira. Kodi mulibe vunguti m'Giliyadi? Kodi mulibe sing'anga m'menemo; analekeranji kuchira mwana wamkazi wa anthu anga? Ha, mutu wanga ukadakhala madzi, ndi maso anga kasupe wa misozi, kuti usana ndi usiku ndilirire ophedwa a mwana wamkazi wa anthu anga! Ha, ndikadakhala ndi chigono cha anthu aulendo m'chipululu; kuti ndisiye anthu anga, ndiwachokere, pakuti onse ali achigololo, msonkhano wa anthu achiwembu. Ndipo apinda lilime lao ngati uta wao, liname; koma akula mphamvu m'dzikomo, koma si pachoonadi; pakuti alinkunkabe nachita zoipa, ndipo sandidziwa Ine, ati Yehova. Muchenjere naye yense mnansi wake, musakhulupirire yense mbale wake; pakuti abale onse amanyenga, ndipo anansi onse adzayenda ndi maugogodi. Ndipo yense adzanyenga mnansi wake, osanena choonadi; aphunzitsa lilime lao kunena zonama; nadzithodwetsa kuchita zoipa. Ukhala pakati pa manyengo m'manyengo; akana kundidziwa, ati Yehova. Chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Taonani, ndidzawasungunula, ndi kuwayesa, pakuti ndidzachitanji, chifukwa cha mwana wamkazi wa anthu anga? Lilime lao ndi muvi wakuphera; linena manyengo; wina anena mtendere ndi mnansi wake pakamwa pake, koma m'mtima mwake amlalira. Kodi sindidzawalanga chifukwa cha izi? Ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera chilango mtundu wotere? Chifukwa cha mapiri ndidzagwa misozi ndi kulira, chifukwa cha mabusa a chipululu ndidzachita maliro, chifukwa apserera, kuti anthu sangathe kupitirirapo; ndiponso anthu sangathe kumva mau a ng'ombe zao; mbalame za mlengalenga ndi nyama zathawa, zapita. Ndipo ndidzayesa Yerusalemu miyulu, mbuto ya ankhandwe; ndipo ndidzayesa midzi ya Yuda bwinja, lopanda wokhalamo. Wanzeru ndani, kuti adziwe ichi? Ndani iye amene kamwa la Yehova lanena naye, kuti achilalikire? Chifukwa chake dziko litha ndi kupsereza monga chipululu, kuti anthu asapitemo? Ndipo Yehova ati, Chifukwa asiya chilamulo changa ndinachiika pamaso pao, ndipo sanamvera mau anga, osayenda m'menemo; koma anatsata kuuma kwa mtima wao, ndi Baala, monga makolo ao anawaphunzitsa; chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Taonani, ndidzadyetsa anthu awa chivumulo, ndi kuwamwetsa madzi andulu. Ndidzawabalalitsanso mwa amitundu, amene iwo kapena makolo ao sanawadziwa; ndipo ndidzatumiza lupanga, liwatsate mpaka ndawatha. Atero Yehova wa makamu, Kumbukirani inu, ndi kuitana akazi akulira, adze; aitaneni akazi ochenjera, kuti adze; afulumire, atikwezere ife mau a maliro, kuti maso athu agwe misozi, ndi zikope zathu ziyendetse madzi. Pakuti mau a kulira amveka m'Ziyoni, Tafunkhidwa, tanyazitsidwa, pakuti tasiya dziko, pakuti agwetsa zokhalamo zathu. Koma imvani mau a Yehova, akazi inu, khutu lanu lilandire mau a pakamwa pake, phunzitsani ana anu akazi kulira, ndi yense aphunzitse mnzake maliridwe ake. Pakuti imfa yakwera m'mazenera athu, yalowa m'nyumba mwathu; kuchotsa ana kubwalo, ndi anyamata kumiseu. Nenani, atero Yehova, Mitembo yathu idzagwa ngati ndowe pamunda, ndi monga chipukutu pambuyo pa wakusenga, palibe wochitola. Atero Yehova, wanzeru asadzitamandire m'nzeru zake, wamphamvu asadzitamandire m'mphamvu yake, wachuma asadzitamandire m'chuma chake; koma wakudzitamandira adzitamandire adzikweze umo, kuti ali wakuzindikira, ndi kundidziwa Ine, kuti ndine Yehova wakuchita zokoma mtima, chiweruziro, ndi chilungamo m'dziko lapansi, pakuti m'menemo ndikondwerera, ati Yehova. Taonani, masiku alikudza, ati Yehova, kuti ndidzalanga onse odulidwa m'kusadulidwa kwao; Ejipito, ndi Yuda, ndi Edomu, ndi ana a Amoni, ndi a Mowabu, ndi onse ometa m'mphepete mwa tsitsi lao, okhala m'chipululu; pakuti amitundu onse ali osadulidwa, ndi nyumba ya Israele ili yosadulidwa m'mtima. Tamvani mau amene Yehova anena kwa inu, nyumba ya Israele; Atero Yehova, Musaphunzire njira ya amitundu, musaope zizindikiro za m'thambo; pakuti amitundu aziopa izo. Pakuti miyambo ya anthu ili yachabe, pakuti wina adula mtengo m'nkhalango, ntchito ya manja a mmisiri ndi nkhwangwa. Aukometsa ndi siliva ndi golide; auchirikiza ndi misomali ndi nyundo, kuti usasunthike. Mafanowa akunga mtengo wakanjedza, wosemasema, koma osalankhula; ayenera awanyamule, pakuti sangathe kuyenda. Musawaope; pakuti sangathe kuchita choipa, mulibenso mwa iwo kuchita chabwino. Chifukwa palibe akunga Inu, Yehova; muli wamkulu, ndipo dzina lanu lili lalikulu ndi lamphamvu. Wosaopa Inu ndani, Mfumu ya amitundu? Pakuti kukuopani ndi kwanu; pakuti mwa anzeru onse a amitundu, ndi m'maufumu ao onse, mulibe akunga Inu. Koma onse pamodzi apulukira ndi kupusa; mtengo ndiwo chilangizo, chopanda pake. Abwera ndi siliva wa ku Tarisisi, wosulasula wopyapyala ndi golide wa ku Ufazi, ntchito ya mmisiri ndi manja a woyenga; zovala zao ndi nsalu ya madzi ndi yofiirira; zonsezi ndi ntchito za muomba. Koma Yehova ndiye Mulungu woona; ndiye Mulungu wamoyo, mfumu yamuyaya; pa mkwiyo wake dziko lapansi lidzanthunthumira, ndi amitundu sangapirire ukali wake. Muzitero nao, milungu imene sinalenga miyamba ndi dziko lapansi, iyo idzatha kudziko lapansi, ndi pansi pa miyambayo. Iye analenga dziko lapansi ndi mphamvu yake, nakhazikitsa dziko lapansi ndi nzeru yake, nayala thambo ndi kuzindikira kwake; polankhula Iye, pali unyinji wa madzi m'mwamba, ndipo akweretsa nkhungu ku malekezero a dziko lapansi, alenga mphezi idzetse mvula, natulutsa mphepo m'zosungira zake. Anthu onse ali opulukira ndi opanda nzeru; woyenga yense anyazitsidwa ndi fanizo lake losemasema; pakuti fanizo lake loyenga lili bodza, mulibe mpweya mwa iwo. Ndiwo chabe, ndiwo chiphamaso; pa nthawi ya kulangidwa kwao adzatha. Gawo la Yakobo silifanana ndi iwo; pakuti Iye ndiye analenga zonse; Israele ndiye mtundu wa cholowa chake; dzina lake ndi Yehova wa makamu. Nyamula katundu wako, iwe wokhala m'linga. Pakuti atero Yehova, Taonani, ndidzaponya kunja okhala m'dziko ili tsopanoli, ndi kuwasautsa, kuti azindikire. Tsoka ine, ndalaswa! Bala langa lindipweteka; koma ine ndinati, Ndithu vuto langa ndi ili, ndipirire nalo. Hema wanga waonongeka, zingwe zanga zonse zaduka; ana anga atuluka mwa ine, palibe iwo; palibenso amene adzamanga hema wanga, kapena kutchinga nsalu zanga. Pakuti abusa apulukira, sanafunsire kwa Yehova; chifukwa chake sanapindule; zoweta zao zonse zabalalika. Mbiri yamveka, taonani ikudza, ndi phokoso lalikulu lituluka m'dziko la kumpoto, likachititse midzi ya Yuda bwinja, ndi mbuto ya nkhandwe. Inu Yehova, ndidziwa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake. Yehova, mundilangize, koma ndi chiweruzo; si m'mkwiyo wanu, mungandithe psiti. Tsanulirani ukali wanu pa amitundu osakudziwani Inu, ndi pa mabanja osaitana dzina lanu; pakuti anadya Yakobo, inde, anamudya namutha, napasula mokhalamo mwake. Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, kuti, Imvani mau a pangano ili, nenani kwa anthu a Yuda, ndi anthu a Yerusalemu; ndi kunena kwa iwo, Atero Yehova, Mulungu wa Aisraele: Wotembereredwa ndi munthu wosamvera mau a pangano ili, limene ndinauza makolo anu tsiku lomwe ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito, m'ng'anjo ya chitsulo, kuti, Mverani mau anga, ndi kuwachita, monga mwa zonse zimene ndikuuzani inu; ndipo mudzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu; kuti ndikalimbikitse lumbiro limene ndinalumbirira makolo anu, ndiwapatse dziko moyenda mkaka ndi uchi, monga lero lomwe. Ndipo ndinayankha, ndi kuti, Amen, Yehova. Ndipo Yehova anati kwa ine, Lalikira mau aonsewa m'midzi ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, kuti, Tamvani mau a pangano ili, ndi kuwachita. Pakuti ndinatsimikizitsa kwa atate anu tsiku lomwe ndinawatulutsa iwo kudziko la Ejipito, mpaka lero lomwe, kuuka mamawa ndi kutsimikiza, kuti, Mverani mau anga. Koma sanamvere, sanatchere khutu lao, koma onse anayenda m'kuumirira kwa mtima wao woipa; chifukwa chake ndinatengera iwo mau onse a pangano ili, limene ndinauza iwo kuti achite, koma sanachite. Ndipo Yehova anati kwa ine, Chiwembu chaoneka mwa anthu a Yuda, ndi mwa anthu okhala m'Yerusalemu. Abwerera kuchitanso zoipa za makolo ao, amene anakana kumva mau anga; ndipo atsata milungu ina kuti aitumikire; nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda zaswa pangano langa limene ndinapangana ndi makolo ao. Chifukwa chake atero Yehova, Taonani, ndidzatengera pa iwo choipa, chimene sangathe kuchipulumuka; ndipo adzandifuulira Ine, koma sindidzamvera iwo. Ndipo midzi ya Yuda ndi okhala m'Yerusalemu adzapita nadzafuulira kwa milungu imene anaifukizira; koma siidzawapulumutsa konse nthawi ya nsautso yao. Pakuti milungu yako ilingana ndi kuchuluka kwa midzi yako, iwe Yuda; ndi maguwa a nsembe amene mwautsira chamanyazi, alingana ndi kuchuluka kwa miseu ya Yerusalemu, ndiwo maguwa akufukizirapo Baala. Chifukwa chake usawapempherere anthu awa, usawakwezere iwo mfuu, kapena pemphero, pakuti sindidzamva iwo nthawi imene andifuulira Ine m'kusauka kwao. Wokondedwa wanga afunanji m'nyumba mwanga, popeza wachita choipa ndi ambiri, ndipo thupi lopatulika lakuchokera iwe? Pamene uchita choipa ukondwera nacho. Yehova anatcha dzina lako, Mtengo wa azitona wauwisi, wokoma wa zipatso zabwino; ndi mau a phokoso lalikulu wayatsa moto pamenepo, ndipo nthambi zake zathyoka. Pakuti Yehova wa makamu, amene anakuoka iwe, wakunenera iwe choipa, chifukwa cha zoipa za nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda, zimene anadzichitira okha pakuutsa mkwiyo wanga m'mene anafukizira Baala. Ndipo Yehova anandidziwitsa, ndipo ndinadziwa; ndipo wandisonyeza ine machitidwe ao. Koma ine ndinanga mwanawankhosa wofatsa wotengedwa kukaphedwa; ndipo sindinadziwa kuti anandichitira ine chiwembu, kuti, Tiononge mtengo ndi zipatso zake, timdule iye pa dziko la amoyo, kuti dzina lake lisakumbukikenso. Koma, Yehova wa makamu, amene aweruza molungama, amene ayesa impso ndi mtima, ndikuoneni Inu mulikuwabwezera chilango, pakuti kwa Inu ndawulula mlandu wanga. Chifukwa chake atero Yehova za anthu a Anatoti, amene afuna moyo wanga, kuti, Usanenere m'dzina la Yehova, ungafe ndi mkono wathu; chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Taonani, ndidzalanga iwo; anyamata adzafa ndi lupanga; ana ao aamuna ndi aakazi adzafa ndi njala; ndipo sadzakhala nao otsalira; pakuti ndidzatengera choipa pa anthu a ku Anatoti, chaka cha kulangidwa kwao. Wolungama ndinu, Yehova, pamene nditsutsana nanu mlandu; pokhapo ndinenane nanu za maweruzo; chifukwa chanji ipindula njira ya oipa? Chifukwa chanji akhala bwino onyengetsa? Inu Mwabzala iwo, inde, anagwiritsatu mizu; amera, inde, abalatu zipatso; muli pafupi m'kamwa mwao, muli patali ndi impso zao. Koma inu, Yehova, mundidziwa ine; mundiona ine, muyesa mtima wanga ngati utani nanu; muwatulutse iwo monga nkhosa za kuphedwa, ndi kuwakonzeratu tsiku lakuphedwa. Dziko lidzalira masiku angati, nilifota therere la minda yonse? Chifukwa cha zoipa za iwo okhalamo, zithedwa zinyama, ndi mbalame; pakuti iwo anati, Iye sadzaona chitsiriziro chathu. Ngati wathamanga pamodzi ndi oyenda pansi, ndipo iwo anakulemetsa iwe, udzayesana nao akavalo bwanji? Ndipo ngakhale ukhazikika m'dziko lamtendere, udzachita chiyani m'kudzikuza kwa Yordani? Pakuti ngakhale abale ako, ndi nyumba ya atate wako, ngakhale iwo anakunyenga iwe; ngakhale anakufuulira iwe; usamvere iwo, ngakhale anena nawe mau abwino. Ndachoka kunyumba yanga, ndasiya cholowa changa; ndapereka wokondedwa wa mtima wanga m'dzanja la adani. Cholowa changa chandisandukira mkango wa m'nkhalango; anatsutsana nane ndi mau ake; chifukwa chake ndinamuda. Cholowa changa chili kwa ine ngati mbalame yamawalamawala yolusa? Kodi mbalame zolusa zimzinga ndi kudana naye? Mukani, musonkhanitse zilombo za m'thengo, mudze nazo zidye. Abusa ambiri aononga munda wanga wamphesa, apondereza gawo langa, pondikondweretsa apayesa chipululu chopanda kanthu. Apayesa bwinja; pandilirira ine, pokhala bwinja; dziko lonse lasanduka bwinja; chifukwa palibe munthu wosamalira. Akufunkha afika pa mapiri oti see m'chipululu; pakuti lupanga la Yehova lilusa kuyambira pa mbali ina ya dziko kufikira kumbali ina; palibe thupi lokhala ndi mtendere. Abzala tirigu, asenga minga; adzipweteka, koma osapindula kanthu, mudzakhala ndi manyazi a zipatso zanu, chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Yehova. Atero Yehova ponenera anansi anga onse oipa, amene akhudza cholowa chimene ndalowetsamo anthu anga Israele; taonani, ndidzazula iwo m'dziko lao, ndipo ndidzazula nyumba ya Yuda pakati pao. Ndipo padzakhala kuti nditazula iwo, ndidzabwera, ndipo ndidzawachitira chisoni; ndipo ndidzabwezanso iwo, yense ku cholowa chake, ndi yense kudziko lake. Ndipo padzakhala kuti, ngati iwo adzaphunzira mwakhama njira za anthu anga, kulumbira ndi dzina langa, Pali Yehova; monga anaphunzitsa anthu anga kulumbira pali Baala; pamenepo ndidzamangitsa mudzi wao pakati pa anthu anga. Koma ngati sakumva, ndidzazula mtundu umene wa anthu, kuuzula ndi kuuononga, ati Yehova. Atero Yehova kwa ine, Pita, udzigulire mpango wabafuta, nudzimangire m'chuuno mwako, usauike m'madzi. Ndipo ndinagula mpango monga mwa mau a Yehova, ndi kuvala m'chuuno mwanga. Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine nthawi yachiwiri, kuti, Tenga mpango umene unaugula, umene uli m'chuuno mwako, nuuke, nupite ku Yufurate, nuubise m'menemo m'phanga la m'mwala. Ndipo ndinapita, ndinaubisa pa Yufurate, monga Yehova anandiuza ine. Ndipo panali atapita masiku ambiri, kuti Yehova anati mwa ine, Uka, pita ku Yufurate, nukatenge kumeneko mpango uja, ndinakuuza iwe ukaubise kumeneko. Ndipo ndinanka ku Yufurate, ndikumba, nditenga mpango m'malo m'mene ndinaubisamo; ndipo, taonani, mpango unaonongeka, wosayenera kanthu. Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, kuti, Yehova atero, Momwemo ndidzaononga kudzitama kwa Yuda, ndi kudzitama kwakukulu kwa Yerusalemu. Anthu oipa awa, amene akana kumva mau anga, amene ayenda m'kuumirira kwa mtima wao, atsata milungu ina kuitumikira, ndi kuigwadira, adzakhala ngati mpango uwu, wosayenera kanthu. Pakuti monga mpango uthina m'chuuno cha munthu, chomwecho ndinathinitsa kwa Ine nyumba yonse ya Israele ndi nyumba yonse ya Yuda, ati Yehova, kuti akhale kwa Ine anthu, ndi dzina, ndi chilemekezo, ndi ulemerero; koma anakana kumva. Chifukwa chake uzinena ndi iwo mau awa: Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Matumba onse adzadzazidwa ndi vinyo; ndipo adzati kwa iwe, Kodi sitidziwitsa bwino kuti matumba onse adzadzazidwa ndi vinyo? Ndipo udzati kwa iwo, Atero Yehova, Taonani, ndidzadzaza ndi chiledzero onse okhala m'dziko muno, ngakhale mafumu onse amene akhala pa mpando wachifumu wa Davide, ndi ansembe, ndi aneneri, ndi onse okhala m'Yerusalemu. Ndipo ndidzaphwanyanitsa wina ndi wina, atate ndi ana, ati Yehova; sindidzakhala ndi chisoni, sindidzapulumutsa, sindidzakhala ndi chifundo, chakuti ndisawaononge. Tamvani inu, Tcherani khutu; musanyade, pakuti Yehova wanena. Lemekezani Yehova Mulungu wanu, kusanade, mapazi anu asanakhumudwe pa mapiri achizirezire; nimusanayembekeze kuunika, Iye asanasandutse kuunikaku mthunzi wa imfa, ndi kukuyesa mdima wa bii. Koma ngati simudzamva, moyo wanga udzalira m'tseri chifukwa cha kunyada kwanu; diso langa lidzalira kwambiri, lidzagwa misozi, chifukwa zoweta za Yehova zagwidwa m'nsinga. Nenani kwa mfumu ndi kwa amake wa mfumu, Dzichepetseni, khalani pansi; pakuti zapamtu zanu zagwa, korona wanu wokoma. Midzi ya kumwera yatsekedwa, palibe wotsegulira. Yuda wonse wachotsedwa m'ndende wonsewo, wachotsedwa m'nsinga. Tukulani maso anu, taonani iwo amene achokera kumpoto; zili kuti zoweta zinapatsidwa kwa iwe, zoweta zako zokoma? Udzanena chiyani pamene adzaika abale ako akulu ako, pakuti iwe wekha wawalangiza iwo akukana iwe? Kodi zowawa sizidzakugwira iwe monga mkazi wobala? Ndipo ngati udzati m'mtima mwako, Zimenezi zandifikira ine chifukwa ninji? Chifukwa cha choipa chako chachikulu nsalu zako zoyesa mfula zasanduka mbudulira, ndi zithende zako zaphwetekwa. Kodi angathe Mkusi kusanduliza khungu lake, kapena nyalugwe mawanga ake? Pamenepo mungathe inunso kuchita zabwino, inu amene muzolowera kuchita zoipa. Chifukwa chake ndidzabalalitsa iwo, monga ziputu zakupita, ndi mphepo ya kuchipululu. Ichi ndi chogwera chako, gawo la muyeso wako wa kwa Ine, ati Yehova; chifukwa wandiiwala Ine, ndi kukhulupirira zonama. Chifukwa chake Ine ndidzaonetsa zotopola mikawo zako, pamaso pako, ndipo manyazi ako adzaoneka. Ndaona zonyansa zako, ndi zigololo zako, ndi zakumemesa zako, ndi chinyerinyeri cha dama lako, pamapiri ndi m'munda. Tsoka kwa iwe, Yerusalemu! Sudzayeretsedwa; kodi zidzatero mpaka liti? Mau a Yehova amene anadza kwa Yeremiya onena za chilala. Yuda alira, ndipo zipata zake zilefuka, zikhala pansi zovekedwa ndi zakuda; mfuu wa Yerusalemu wakwera. Akulu ao atuma ang'ono ao kumadzi; afika kumaenje, osapeza madzi; abwera ndi mitsuko yao yopanda kanthu; ali ndi manyazi, athedwa nzeru, afunda mitu yao. Chifukwa cha nthaka yochita ming'alu, pakuti panalibe mvula padziko, olima ali ndi manyazi, afunda mitu yao. Inde, mbawalanso ya m'thengo ibala nisiya ana ake, chifukwa mulibe udzu. Mbidzi zinaima pamapiri oti see, zipumira mphepo wefuwefu ngati ankhandwe; maso ao alema, chifukwa palibe udzu. Zingakhale zoipa zathu zititsutsa ife, chitani Inu chifukwa cha dzina lanu, Yehova; pakuti zobwerera zathu zachuluka; takuchimwirani Inu. Inu, chiyembekezo cha Israele, Mpulumutsi wake nthawi ya msauko, bwanji mukhala ngati mlendo m'dziko, ngati woyendayenda amene apatuka usiku? Bwanji mukhala ngati munthu wodabwa, ngati munthu wamphamvu wosatha kupulumutsa? Koma Inu, Yehova, muli pakati pathu, titchedwa ndi dzina lanu; musatisiye. Atero Yehova kwa anthu awa, Chomwecho akonda kusocherera; sanakanize mapazi ao; chifukwa chake Yehova sawalandira; tsopano adzakumbukira choipa chao, nadzalanga zochimwa zao. Ndipo Yehova anati kwa ine, Usapempherere anthu awa zabwino. Pamene asala chakudya, sindidzamva kufuula kwao; ndipo pamene apereka nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa sindidzawalandira; koma ndidzawatha ndi lupanga, ndi chilala, ndi chaola. Ndipo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! Taonani, aneneri ati kwa iwo, Simudzaona lupanga, simudzakhala ndi chilala; koma ndidzakupatsani mtendere weniweni mommuno. Ndipo Yehova anati kwa ine, Aneneri anenera zonama m'dzina langa; sindinatuma iwo, sindinauza iwo, sindinanena nao; anenera kwa inu masomphenya onama, ndi ula, ndi chinthu chachabe, ndi chinyengo cha mtima wao. Chifukwa chake atero Yehova za aneneri onenera m'dzina langa, ndipo sindinawatuma, koma ati, Lupanga ndi chilala sizidzakhala m'dziko muno; ndi lupanga ndi chilala aneneriwo adzathedwa. Ndipo anthu amene adzanenera kwa inu adzaponyedwa kunja m'miseu ya Yerusalemu chifukwa cha chilala ndi lupanga; ndipo adzasowa akuwaika, ndi akazi ao, ndi ana ao aamuna ndi aakazi; ndipo ndidzatsanulira pa iwo zoipa zao. Ndipo udzati kwa iwo mau awa, Maso anga agwe misozi usana ndi usiku, asaleke; pakuti namwali mwana wa anthu anga wasweka ndi kusweka kwakukulu, ndi bala lopweteka kwambiri. Ndikatulukira kumunda, taonani ophedwa ndi lupanga! Ndikalowa m'mudzi, taonani odwala ndi njala! Pakuti mneneri ndi wansembe ayendayenda m'dziko osadziwa kanthu. Kodi mwakanadi Yuda? Kodi mtima wanu wanyansidwa ndi Ziyoni? Bwanji mwatipanda ife, ndipo tilibe kuchira? Tinayembekeza mtendere, koma sizinafike zabwino; tinayembekeza nthawi yakuchira, ndipo taonani mantha! Tivomereza, Yehova, chisalungamo chathu, ndi choipa cha makolo athu; pakuti takuchimwirani Inu. Musatinyoze ife, chifukwa cha dzina lanu; musanyazitse mpando wachifumu wa ulemerero wanu; mukumbukire musasiye pangano lanu lopangana ndi ife. Mwa zachabe za mitundu ya anthu zilipo kodi, zimene zingathe kuvumbitsa mvula? Kodi si ndinu, Yehova, Mulungu wathu? Ndipo tidzakudikirani Inu; pakuti munalenga zonse zimenezi. Ndipo Yehova anati kwa ine, Ngakhale Mose ndi Samuele akadaima pamaso panga, koma mtima wanga sukadasamalira anthu awa; muwachotse iwo pamaso panga, atuluke. Ndipo padzakhala, pamene adzati kwa iwe, Titulukire kuti? Pamenepo uziti, Atero Yehova: Amene a kuimfa, anke kuimfa; amene a kulupanga, anke kulupanga; amene a kunjala, anke kunjala; ndi amene a kunsinga, anke kunsinga. Ndipo ndidzaika pa iwo mitundu inai, ati Yehova, lupanga lakupha, agalu akung'amba, mbalame za m'mlengalenga, ndi zilombo zapansi, zakulusa ndi kuononga. Ndipo ndidzawapereka akhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko lapansi, chifukwa cha Manase mwana wa Hezekiya mfumu ya Yuda, chifukwa cha zija anachita m'Yerusalemu. Pakuti ndani adzakuchitira iwe chisoni, Yerusalemu? Ndani adzakulirira iwe? Ndani adzapatukira kudzafunsa za mkhalidwe wako? Iwe wandikana Ine, ati Yehova, wabwerera m'mbuyo; chifukwa chake ndatambasulira dzanja langa pa iwe, ndi kukuononga iwe; ndatopa ndi kulekerera. Ndawapeta ndi chopetera m'zipata za dziko; ndachotsa ana ao, ndasakaza anthu anga; sanabwerere kuleka njira zao. Amasiye ao andichulukira Ine kopambana mchenga wa kunyanja; ndatengera wofunkha usana afunkhire mai wao wa anyamata; ndamgwetsera dzidzidzi kuwawa mtima ndi mantha. Mkazi amene anabala asanu ndi awiri walefuka; wapereka moyo; dzuwa lake lalowa usana ulipobe; wanyazitsidwa, wathedwa nzeru; otsala ao ndidzapereka kulupanga pamaso pa adani ao, ati Yehova. Kalanga ine, amai, pakuti mwandibala ine munthu wandeu, munthu wakutetana nalo dziko lonse lapansi! Sindinakongoletsa paphindu, anthu sanandikongoletse paphindu; koma iwo onse anditemberera. Yehova anati, Ndithu ndidzakulimbitsira iwe zabwino; ndithu ndidzapembedzetsa mdani kwa iwe nthawi ya zoipa ndi nthawi ya nsautso. Kodi angathe munthu kuthyola chitsulo, chitsulo cha kumpoto, ndi mkuwa? Chuma chako ndi zosungidwa zako ndidzazipereka zifunkhidwe kopanda mtengo wake, ichicho chidzakugwera chifukwa cha zochimwa zako zonse, m'malire ako onse. Ndipo ndidzawapititsa iwo pamodzi ndi adani ako kudziko limene sudziwa iwe; pakuti moto wayaka m'mkwiyo wanga, umene udzatentha inu. Inu Yehova, mudziwa; mundikumbukire ine, mundiyang'anire Ine, mundibwezere chilango pa ondisautsa ine; musandichotse m'chipiriro chanu; dziwani kuti chifukwa cha Inu ndanyozedwa. Mau anu anapezeka, ndipo ndinawadya; mau anu anakhala kwa ine chikondwero ndi chisangalalo cha mtima wanga; pakuti ndatchedwa dzina lanu, Yehova Mulungu wa makamu. Sindinakhala m'msonkhano wa iwo amene asekerasekera, ndi kusangalala; ndinakhala pandekha chifukwa cha dzanja lanu; pakuti mwandidzaza ndi mkwiyo. Kupweteka kwanga kuli chipwetekere bwanji, ndi bala langa losapoleka, likana kupola? Kodi mudzakhala kwa ine ngati kamtsinje konyenga, ngati madzi omwerera? Chifukwa chake atero Yehova, Ukabwerera pamenepo ndidzakubwezanso, kuti uime pamaso panga; ndipo ukasiyanitsa cha mtengo wake ndi chonyansa, udzakhala ngati m'kamwa mwanga; ndipo adzabwerera kwa iwe, koma sudzabwerera kwa iwo. Ndidzakuyesa iwe linga lamkuwa la anthu awa; ndipo adzamenyana ndi iwe, koma iwo sadzakuposa iwe; pakuti Ine ndili ndi iwe kuti ndikupulumutse ndi kukulanditsa iwe, ati Yehova. Ndipo ndidzakulanditsa iwe m'dzanja la oipa, ndipo ndidzakuombola iwe m'dzanja la oopsa. Ndiponso mau a Yehova anadza kwa ine, kuti, Usatenge mkazi, usakhale ndi ana aamuna ndi aakazi m'malo muno. Pakuti Yehova atero za ana amuna ndi za ana akazi akubadwa m'malo muno, ndi za amai anawabala iwo, ndi za atate ao anawabala iwo m'dziko muno: Adzafa ndi imfa zanthenda; sadzaliridwa maliro, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka; ndipo adzathedwa lupanga, ndi njala; ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame za kumlengalenga, ndi zilombo za dziko lapansi. Pakuti Yehova atero, Usalowe m'nyumba ya maliro, usanke kukachita maliro ao, kapena kuwalirira; pakuti ndachotsa mtendere wanga pa anthu awa, chifundo ndi nsoni zokoma, ati Yehova. Akulu ndi ang'onong'ono adzafa m'dziko muno; sadzaikidwa, anthu sadzachita maliro ao, sadzadzicheka, sadzadziyeseza adazi, chifukwa cha iwo; anthu sadzawagawira mkate pamaliro, kuti atonthoze mitima yao chifukwa cha akufa, anthu sadzapatsa iwo chikho cha kutonthoza kuti achimwe chifukwa cha atate ao kapena mai wao. Usalowe m'nyumba ya madyerero kukhala nao, ndi kudya ndi kumwa. Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele; Taonani, ndidzaletsa pano, pamaso panu masiku anu, mau akukondwerera ndi mau akusangalala, mau a mkwati ndi mau a mkwitibwi. Ndipo padzakhala, pamene udzaonetsa anthu awa mau awa onse, ndipo iwo adzati kwa iwe, Chifukwa chake nchiyani kuti Yehova watinenera ife choipa chachikulu ichi? Mphulupulu yathu ndi yanji? Tchimo lathu lanji limene tachimwira Yehova Mulungu wathu? Pamenepo uziti kwa iwo, Chifukwa makolo anu anandisiya Ine, ati Yehova, natsata milungu ina, naitumikira, naigwadira, nandisiya Ine, osasunga chilamulo changa; ndipo mwachita zoipa zopambana makolo anu; pakuti, taonani, muyenda yense potsata kuumirira kwa mtima wake woipa, kuti musandimvere Ine; chifukwa chake ndidzakutulutsani inu m'dziko muno munke kudziko limene simunadziwa, kapena inu kapena makolo anu; pamenepo mudzatumikira milungu ina usana ndi usiku, kumene sindidzachitira inu chifundo. Chifukwa chake, taonani, masiku adza, ati Yehova, kuti sadzanenanso, Pali Yehova, amene anakweza ana a Israele kuwatulutsa m'dziko la Ejipito. Koma, Pali Yehova, amene anakweza ana a Israele kuchokera kudziko la kumpoto, ndi kumaiko ena kumene anawapirikitsirako; ndipo ndidzawabwezanso kudziko lao limene ndinapatsa makolo ao. Taonani, ndidzaitana akugwira nsomba ambiri, ati Yehova, ndipo adzawagwira iwo, pambuyo pake ndidzaitana osaka nyama ambiri, ndipo adzasaka iwo m'mapiri onse, ndi pa zitunda zonse, ndiponso m'mapanga a m'matanthwe. Pakuti maso anga ali pa njira zao zonse, sabisika pa nkhope yanga, mphulupulu yao siibisika pamaso panga. Poyamba ndibwezera mphulupulu yao ndi tchimo lao chowirikiza; chifukwa anaipitsa dziko langa ndi mitembo ya zodetsedwa zao, nadzaza cholowa changa ndi zonyansa zao. Inu Yehova, mphamvu yanga, ndi linga langa, pothawirapo panga tsiku la msauko, amitundu adzadza kwa Inu kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, ndipo adzati, Makolo athu analandira cholowa cha bodza lokha, zopanda pake ndi zinthu zosapindula nazo. Kodi munthu adzadzipangira yekha milungu, imene siili milungu? Chifukwa chake, taonani, ndidzadziwitsa iwo kamodzi aka, ndidzawadziwitsa dzanja langa ndi mphamvu yanga; ndipo adzadziwa kuti dzina langa ndine Yehova. Tchimo la Yuda lalembedwa ndi peni lachitsulo, ndi nsonga ya diamondi; lalembedwa pa cholembapo cha m'mtima mwao, ndi pa nyanga za maguwa a nsembe anu. Pokumbukira ana ao maguwa a nsembe ao ndi zoimiritsa zao kumitengo yaiwisi ya pa zitunda zazitali. Iwe phiri langa la m'munda, ndidzapereka chuma chako ndi zosungidwa zako zikafunkhidwe, ndi misanje yako, chifukwa cha tchimo, m'malire ako onse. Iwe, iwe wekha, udzaleka pa cholowa chako chimene ndinakupatsa iwe; ndipo ndidzakutumikiritsa adani ako m'dziko limene sulidziwa; pakuti wakoleza moto m'mkwiyo wanga umene udzatentha kunthawi zamuyaya. Atero Yehova: Wotembereredwa munthu amene akhulupirira munthu, natama mkono wanyama, nuchoka kwa Yehova mtima wake. Ndipo adzakhala ngati tsanya la m'chipululu, ndipo saona pamene chifika chabwino; koma adzakhala m'malo oumitsa m'chipululu, dziko lachikungu lopanda anthu. Wodala munthu amene akhulupirira Yehova, amene chikhulupiriro chake ndi Yehova. Ndipo adzakhala ngati mtengo wooka kuli madzi, wotambalitsa mizu yake pamtsinje, wosaopa pofika nyengo yadzuwa, koma tsamba lake likhala laliwiri; ndipo suvutika chaka cha chilala, suleka kubala zipatso. Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika, ndani angathe kuudziwa? Ine Yehova ndisanthula mtima, ndiyesa impso, kuti ndimpatse munthu yense monga mwa njira zake, monga zipatso za ntchito zake. Monga nkhwali iumatira pa mazira amene sinaikira, momwemo iye amene asonkhanitsa chuma, koma mosalungama; pakati pa masiku ake chidzamsiya iye, ndipo pa chitsirizo adzakhala wopusa. Malo opatulika athu ndiwo mpando wachifumu wa ulemerero, wokhazikika pamsanje chiyambire. Inu Yehova, chiyembekezo cha Israele, onse amene akukusiyani Inu adzakhala ndi manyazi; onse ondichokera Ine adzalembedwa m'dothi, chifukwa asiya Yehova, kasupe wa madzi amoyo. Mundichiritse ine, Yehova, ndipo ndidzachiritsidwa; mundipulumutse ine, ndipo ndidzapulumutsidwa; pakuti chilemekezo changa ndinu. Taonani, ati kwa ine, Mau a Yehova ali kuti? Adze tsopano. Koma ine, pokhala mbusa sindinafulumira kuchokerako kuti ndikutsateni Inu; sindinakhumba tsiku la tsoka; Inu mudziwa, chimene chinatuluka pa milomo yanga chinali pamaso panu. Musakhale wondiopsetsa ine; ndinu pothawira panga tsiku la choipa. Iwo akhale ndi manyazi amene andisautsa ine, koma ine ndisakhale ndi manyazi; aopsedwe iwo, koma ndisaopsedwe ine; muwatengere iwo tsiku la choipa, muwaononge ndi chionongeko chowirikiza. Yehova anatero kwa ine: Pita, nuime m'chipata cha ana a anthu, m'mene alowamo mafumu a Yuda, ndi m'mene atulukamo, ndi m'zipata zonse za Yerusalemu; ndipo uziti kwa iwo, Tamvani mau a Yehova, inu mafumu a Yuda, ndi Ayuda onse, ndi onse okhala m'Yerusalemu, amene alowa pa zipatazi; atero Yehova: Tadzayang'anirani nokha, musanyamule katundu tsiku la Sabata, musalowe naye pa zipata za Yerusalemu; musatulutse katundu m'nyumba zanu tsiku la Sabata, musagwire ntchito ili onse; koma mupatule tsiku la Sabata, monga ndinauza makolo anu; koma sanamvere, sanatchere khutu lao, koma anaumitsa khosi lao, kuti asamve asalandire langizo. Ndipo padzakhala, ngati mundimveretsa Ine, ati Yehova, kuti musalowetse katundu pa zipata za mudzi uwu tsiku la Sabata, koma mupatule tsiku la Sabata, osagwira ntchito m'menemo; pamenepo padzalowa pa zipata za mudzi uwu mafumu ndi akulu okhala pa mpando wachifumu wa Davide, okwera pa magaleta ndi akavalo, iwo, ndi akulu ao, anthu a Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu; ndipo mudzi uwu udzakhala kunthawi zamuyaya. Ndipo adzachokera kumidzi ya Yuda, ndi kumalo akuzungulira Yerusalemu, ndi kudziko la Benjamini, ndi kuchidikha, ndi kumapiri, ndi kumwera, ndi kudza nazo nsembe zopsereza, ndi nsembe zophera, ndi nsembe zaufa, ndi lubani, ndi kudza nazo zamayamikiro, kunyumba ya Yehova. Koma ngati simudzamvera Ine kulipatula tsiku la Sabata, kusanyamula katundu ndi kulowa pa zipata za Yerusalemu tsiku la Sabata; pamenepo ndidzayatsa moto m'zipata zakezo, ndipo udzatha zinyumba za Yerusalemu, osazimidwanso. Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, kuti, Tauka, tatsikira kunyumba ya woumba, pamenepo ndidzakumvetsa mau anga. Ndipo ndinatsikira kunyumba ya woumba, ndipo, taonani, anaumba ntchito yake ndi njinga. Ndipo pamene mbiya alikuiumba ndi dothi inaonongeka m'dzanja la woumba, anaiumbanso mbiya ina, monga kunamkomera woumba kuiumba. Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, kuti, Nyumba ya Israele inu, kodi sindingathe kuchita ndi inu monga woumba uyu? Ati Yehova. Taonani, monga dothi m'dzanja la woumba, momwemo inu m'dzanja langa, nyumba ya Israele. Mphindi imene ndidzanena za mtundu wa anthu, kapena za ufumu, kuti ndizule ndi kupasula ndi kuononga; ngati mtundu umene, ndaunenera, udzatembenuka kuleka choipa chao, ndidzaleka choipacho ndidati ndiwachitire. Ndipo mphindi imene ndikanenera mtundu, ndi ufumu, kuti ndimangitse mudzi wake ndi kuuoka; koma ukachita choipa pamaso panga, osamvera mau anga, pamenepo ndidzaleka chabwinocho, ndidati ndiwachitire. Tsopano nenatu kwa anthu a Yuda, ndi kwa okhala m'Yerusalemu, kuti, Atero Yehova: Taonani, Ine ndipangira inu choipa, ndilingalira inu kanthu kakuchitira inu choipa; mubwerere tsono inu nonse, yense kunjira yake yoipa, nimukonze njira zanu ndi machitidwe anu. Koma iwo ati, Palibe chiyembekezero; pakuti ife tidzatsata zilingaliro zathu, ndipo tidzachita yense monga mwa kuuma kwa mtima wake woipa. Chifukwa chake atero Yehova; Funsanitu m'mitundu, ndani wamva zotero; namwali wa Israele wachita chinthu choopsetsa kwambiri. Kodi matalala a Lebanoni adzalephera pa mwala wa m'munda? Kodi adzaphwa madzi ozizira otsika kutali? Pakuti anthu anga andiiwala Ine, afukizira zopanda pake; aphunthwitsa iwo m'njira zao, m'njira zakale, kuti ayende m'njira za m'mbali, m'njira yosatundumuka; kuti aliyense dziko lao likhale lodabwitsa, ndi kutsonya chitsonyere; yense wakupitapo adzadabwa, ndi kupukusa mutu wake. Ndidzamwazamwaza iwo monga ndi mphepo ya kum'mawa pamaso pa adani; ndidzayang'anira pamsana pao, si nkhope yao, tsiku la Tsoka lao. Ndipo iwo anati, Tiyeni, tilingalire Yeremiya chomchitira choipa; pakuti chilamulo sichidzathera wansembe, kapena uphungu wanzeru, kapena mau mneneri. Tiyeni, timpande iye ndi lilime, tisamvere iye mau ake ali onse. Mundimvere ine, Yehova, mumve mau a iwo akulimbana ndi ine. Kodi choipa chibwezedwe pa chabwino? Pakuti akumbira moyo wanga dzenje. Mukumbukire kuti ndinaima pamaso panu kuwanenera zabwino, kuwachotsera iwo ukali wanu. Chifukwa chake mupereke ana ao kunjala, mupereke iwo kumphamvu ya lupanga; akazi ao akhale opanda ana, ndi amasiye; amuna ao aphedwe ndi imfa, ndi anyamata ao apandidwe ndi lupanga kunkhondo. Mfuu umvekedwe m'nyumba zao, pamene muwatengera khamu la nkhondo dzidzidzi; pakuti akumba dzenje lakundigwira ine, anabisira mapazi anga misampha. Koma, Yehova, mudziwa uphungu wao wonse wakundinenera ine kundipha ine; musakhulukire mphulupulu yao, musafafanize tchimo lao pamaso panu; aphunthwitsidwe pamaso panu; muchite nao m'nthawi ya mkwiyo wanu. Atero Yehova, Pita, nugule nsupa ya woumba, nutenge akulu a anthu, ndi akulu a ansembe; nutulukire kuchigwa cha mwana wake wa Hinomu, chimene chili pa khomo la chipata cha mapale, nulalikire kumeneko mau amene ndidzakuuza iwe; nuti, Tamvani mau a Yehova, inu mafumu a Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu; Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzatengera malo ano choipa, chimene aliyense adzachimva, makutu ake adzachita woo. Chifukwa andisiya Ine, nayesa malo ano achilendo, nafukizira m'menemo milungu ina, imene sanaidziwe, iwowa, ndi makolo ao ndi mafumu a Yuda; nadzaza malo ano ndi mwazi wa osachimwa; namanga misanje ya Baala, kuti apsereze ana ao m'menemo nsembe zopsereza za Baala, chimene sindinawauza, sindinachinena, sichinalowa m'mtima mwanga; chifukwa chake, taonani, masiku adza, ati Yehova kuti pamalo pano sipadzatchedwanso Tofeti, kapena Chigwa cha mwana wake wa Hinomu, koma Chigwa Chophera anthu. Ndipo ndidzataya uphungu wa Yuda ndi wa Yerusalemu m'malo ano; ndipo ndidzagwetsa iwo ndi lupanga pamaso pa adani ao, ndi pa dzanja la iwo amene afuna moyo wao; mitembo yao ndidzapatsa ikhale chakudya cha mbalame za m'mlengalenga, ndi cha zilombo za dziko lapansi. Ndipo ndidzayesa mudziwu chodabwitsa, ndi chotsonyetsa; onse amene adzapitapo adzadabwa ndi kutsonya chifukwa cha zopanda pake zonse. Ndipo ndidzadyetsa iwo mnofu wa ana ao aamuna ndi aakazi, ndipo adzadya yense mnofu wa mbale wake, m'nkhondo yozinga ndi m'kupsinjikako, kumene adani ao, ndi iwo akufuna moyo wao, adzapsinja iwo nako. Pamenepo uziphwanya nsupa pamaso pa anthu otsagana ndi iwe, nuziti kwa iwo, Yehova wa makamu atero: Chomwecho ndidzaphwanya anthu awa ndi mudzi uwu, monga aphwanya mbiya ya woumba, imene sangathe kuiumbanso, ndipo adzaika maliro m'Tofeti, mpaka mulibe malo akuikamo. Ndidzatero ndi malo ano, ati Yehova, ndi okhalamo, kusanduliza mudzi uwu ngati Tofeti; ndi nyumba za Yerusalemu, ndi nyumba za mafumu a Yuda, zimene ziipitsidwa, zidzanga malo a Tofeti, ndizo nyumba zonse anafukizira khamu lonse la kumwamba pa matsindwi ao, ndi kuithirira milungu ina nsembe zothira. Pamenepo Yeremiya anadza kuchokera ku Tofeti, kumene Yehova anamtuma iye kuti anenere; ndipo anaima m'bwalo la nyumba ya Yehova, nati kwa anthu onse: Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzatengera mudzi uwu ndi midzi yake yonse choipa chonse chimene ndaunenera; chifukwa anaumitsa khosi lao, kuti asamve mau anga. Ndipo Pasuri mwana wake wa Imeri wansembe, amene anali kapitao wamkulu m'nyumba ya Yehova, anamva Yeremiya alikunenera zimenezi. Ndipo Pasuri anampanda Yeremiya mneneriyo, namuika matangadza amene anali m'chipata cha kumtunda cha Benjamini, chimene chinali kunyumba ya Yehova. Ndipo panali m'mawa mwake, kuti Pasuri anatulutsa Yeremiya m'matangadzamo. Ndipo Yeremiya anati kwa iye, Yehova sanatche dzina lako Pasuri, koma Magorimisabibu. Pakuti Yehova atero, Taonani, ndidzakuyesa iwe choopsa cha kwa iwe mwini, ndi kwa abwenzi ako onse; ndipo iwo adzagwa ndi lupanga la adani ao, ndipo maso ako adzaona; ndipo ndidzapereka Ayuda onse m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzawatengera iwo am'nsinga ku Babiloni, nadzawapha ndi lupanga. Ndiponso ndidzapereka chuma chonse cha mudzi uwu, ndi zaphindu zake zonse, ndi zinthu zake zonse za mtengo wake, inde, zolemera zonse za mafumu a Yuda ndidzapereka m'manja mwa adani ao, amene adzazifunkha, nadzazitenga kunka nazo ku Babiloni. Ndipo iwe, Pasuri, ndi onse okhala m'nyumba mwako mudzanka kundende; ndipo udzafika ku Babiloni, ndi pamenepo udzafa, ndi pamenepo udzaikidwa, iwe, ndi mabwenzi ako onse, amene unawanenera mabodza. Yehova, mwandikopa ine, ndipo ndinakopedwa; muli ndi mphamvu koposa ine, ndipo mwalakika; ine ndikhala choseketsa dzuwa lonse, onse andiseka. Pakuti paliponse ndinena, ndifuula; ndifuula, Chiwawa ndi chofunkha; pakuti mau a Yehova ayesedwa kwa ine chitonzo, ndi choseketsa, dzuwa lonse. Ndipo ngati nditi, Sindidzamtchula Iye, sindidzanenanso m'dzina lake, pamenepo m'mtima mwanga muli ngati moto wotentha wotsekedwa m'mafupa anga, ndipo ndalema ndi kupirira, sindingathe kupiriranso. Pakuti ndamva kugogodera kwa ambiri, mantha pozungulira ponse. Neneza, ndipo tidzamneneza iye, ati atsamwali anga onse, amene ayang'anira kutsimphina kwanga; kapena adzakopedwa, ndipo ife tidzamlaka iye, ndipo tidzambwezera chilango. Koma Yehova ali ndi ine ngati wamphamvu ndi woopsa; chifukwa chake ondisautsa adzaphunthwa, sadzandilala; adzakhala ndi manyazi ambiri, chifukwa sanachite chanzeru, ngakhale ndi kunyazitsa kwamuyaya kumene sikudzaiwalika. Koma, Inu Yehova wa makamu, amene muyesa olungama, amene muona impso ndi mtima, mundionetse ine kubwezera chilango kwanu pa iwo; pakuti kwa inu ndaululira mlandu wanga. Muimbire Yehova, mulemekeze Yehova; pakuti walanditsa moyo wa aumphawi m'dzanja la ochita zoipa. Litembereredwe tsiku limene ndinabadwa; lisadalitsike tsiku limene amai wanga anandibala ine. Atembereredwe munthu amene anatengera mau kwa atate wanga, kuti, Mwana wamwamuna anakubadwira iwe; ndi kumsekeretsatu iye. Munthuyo akhale ngati midzi imene Yehova anapasula, osalekerera; amve mfuu mamawa, ndi mkuwo pausana; chifukwa sanandiphe ine m'mimba; kuti mai wanga akhale manda anga, ndi mimba yake yaikulu nthawi zonse. Chifukwa chanji ndinatuluka m'mimba kuti ndione kutopa ndi kulira, kuti masiku anga athe ndi manyazi? Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, pamene Zedekiya mfumu anatuma kwa iye Pasuri mwana wa Malikiya, ndi Zefaniya mwana wake wa Maaseiya wansembe, akati, Tifunsirenitu ife kwa Yehova; pakuti Nebukadinezara mfumu wa ku Babiloni atithira ife nkhondo; kapena Yehova adzatichitira ife monga mwa ntchito zake zolapitsa, kuti atichokere. Ndipo Yeremiya anati kwa iwo, Muzitero kwa Zedekiya: Yehova, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzabweza zida za nkhondo zimene zili m'manja anu, zimene mumenyana nazo ndi mfumu ya ku Babiloni, ndi Ababiloni akuzinga inu, kunja kwa malinga, ndipo ndidzazisonkhanitsa pakati pa mudzi uwu. Ndipo Ine mwini ndidzamenyana ndi inu ndi dzanja lotambasuka ndi mkono wamphamvu, m'mkwiyo, ndi m'kupsa mtima, ndi m'ukali waukulu. Ndipo ndidzakantha okhalamo m'mudzi uwu, anthu ndi nyama, adzafa ndi chaola chachikulu. Ndipo pambuyo pake, ati Yehova, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi atumiki ake, ndi anthu, ngakhale a m'mudzi uwu amene asiyidwa ndi chaola, ndi lupanga, ndi njala, m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndi m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la amene afuna moyo wao; ndipo adzawakantha ndi lupanga lakuthwa; osawaleka, osachita chisoni, osachita chifundo. Ndipo uziti kwa anthu awa, Yehova atero, Taonani, ndaika pamaso panu njira ya moyo ndi njira ya imfa. Iye amene akhala m'mudzi uwu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi chaola; koma iye amene atuluka, napandukira kwa Ababiloni akuzinga inu, adzakhala ndi moyo, ndipo moyo wake udzapatsidwa kwa iye ngati chofunkha. Pakuti ndaika nkhope yanga pa mudzi uwu ndiuchitire choipa, si chabwino, ati Yehova; ndipo udzapatsidwa m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzautentha ndi moto. Ndipo za nyumba ya mfumu ya Yuda, tamvani mau a Yehova: Nyumba ya Davide iwe, Yehova atero, Chita chiweruzo m'mawa, ndi kumlanditsa amene afunkhidwa m'dzanja la wosautsa, kungatuluke kupsa mtima kwanga ngati moto, ndi kutentha kosazimika, chifukwa cha ntchito zanu zoipa. Taonani, Ine ndine mdani wako, iwe wokhala m'chigwa, ndi pa thanthwe la m'chidikha, ati Yehova; inu amene muti, Ndani adzatsikira kumenyana ndi ife? Ndani adzalowa m'zokhalamo zathu? Ndipo ndidzakulangani inu monga mwa chipatso cha ntchito zanu, ati Yehova; ndipo ndidzayatsa moto m'nkhalango mwake, ndipo udzatha zonse zomzungulira iye. Yehova atero: Tsikira kunyumba ya mfumu ya Yuda, ndi kunena komweko mau awa, ndi kuti, Tamvani mau a Yehova, Inu mfumu ya Yuda, amene mukhala pa mpando wa Davide, inu, ndi atumiki anu, ndi anthu anu amene alowa pa zipata izi. Yehova atero: Chitani chiweruzo ndi chilungamo, landitsani ofunkhidwa m'dzanja la wosautsa; musachite choipa, musamchitire mlendo chiwawa, kapena ana amasiye, kapena akazi amasiye, musakhetse mwazi wosachimwa pamalo pano. Pakuti ngati mudzachitadi ichi pamenepo, padzalowa pa zipata za nyumba iyi mafumu okhala pa mpando wachifumu wa Davide, okwera m'magaleta ndi pa akavalo, iye, ndi atumiki ake, ndi anthu ake. Koma ngati simudzamva mau amenewa, Ine ndilumbira, pali Ine mwini, ati Yehova, nyumba iyi idzakhala yabwinja. Pakuti Yehova atero za nyumba ya mfumu ya Yuda: Ndikuyesa iwe Giliyadi, ndi mutu wa Lebanoni; koma ndidzakuyesa iwe chipululu, ndi midzi yosakhalamo anthu. Ndipo ndidzakupangiratu iwe opasula, yense ndi zida zake; ndipo adzadula mikungudza yako yosankhika nadzaiponya m'moto. Ndipo amitundu ambiri adzapita pa mudzi uwu, nadzati yense kwa mnzake, Yehova anatero nao mudzi waukulu uwu chifukwa ninji? Ndipo adzayankha, Chifukwa anasiya pangano la Yehova Mulungu wao, ndi kugwadira milungu ina, ndi kuitumikira. Musamlirire wakufa, musachite maliro ake; koma mumliritse iye amene amuka, pakuti sadzabweranso, kapena kuonanso dziko la kwao. Pakuti Yehova atero za Salumu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, amene analamulira m'malo mwake mwa Yosiya atate wake, amene anatuluka m'malo muno: Sadzabweranso kuno nthawi iliyonse; koma kumene anamtengera iye ndende, kumeneko adzafa, ndipo sadzaonanso dziko ili. Tsoka iye amene amanga nyumba yake ndi chisalungamo, ndi zipinda zapamwamba ndi chosaweruza bwino; amene agwiritsa mnzake ntchito osamlipira, osampatsa mphotho yake; amene ati, Ndidzadzimangira ndekha nyumba yotakata ndi zipinda zapamwamba zazikulu, nadziboolera mazenera; navundikira chindwi lam'kati ndi mikungudza, naipaka ndi utoto wofiira. Kodi udzakhala mfumu, chifukwa iwe uyesa kuposa ena ndi mikungudza? Kodi atate wako sanadye ndi kumwa, ndi kuweruza molungama? Kumeneko kunamkomera. Iye anaweruza mlandu wa aumphawi ndi osowa; kumeneko kunali kwabwino. Kodi kumeneko si kundidziwa Ine? Ati Ambuye. Koma maso ako ndi mtima wako sizisamalira kanthu koma kusirira, ndi kukhetsa mwazi wosachimwa, ndi kusautsa, ndi zachiwawa, kuti uzichite. Chifukwa chake Yehova atero za Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda: Sadzamlira iye, kuti, Kalanga ine mbale wanga! Kapena, Kalanga ine mlongo wanga! Sadzamlira, kuti, Kalanga ine mbuye! Kapena, Kalanga ine ulemerero wake! Adzamuika monga kuika bulu, adzamkoka nadzamponya kunja kwa zipata za Yerusalemu. Kwera ku Lebanoni, nufuule; kweza mau ako m'Basani; nufuule m'Abarimu; pakuti mabwenzi ako onse atha. Ndinanena ndi iwe m'phindu lako; koma unati, Sindidzamva. Awa ndi makhalidwe ako kuyambira ubwana wako, kuti sudamvera mau anga. Mphepo idzadyetsa abusa ako onse, ndipo mabwenzi ako adzalowa m'ndende; ntheradi udzakhala ndi manyazi ndi kunyazitsidwa chifukwa cha choipa chako chonse. Iwe wokhala m'Lebanoni, womanga chisa chako m'mikungudza, udzachitidwa chisoni chachikulu nanga pamene mapweteko adzadza kwa iwe, monga mkazi alinkudwala! Pali Ine, ati Yehova, ngakhale Koniya mwana wake wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda akadakhala mphete ya pa dzanja langa lamanja, ndikadachotsa iwe kumeneko; ndipo ndidzakupereka iwe m'dzanja la iwo amene afuna moyo wako, m'dzanja la iwo amene uwaopa, m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, m'dzanja la Ababiloni. Ndipo ndidzakutulutsa iwe, ndi mai wako wakubala iwe, kulowa m'dziko lina, limene sunabadwiramo; m'menemo udzafa. Koma kudziko kumene moyo wao ukhumba kubwerera, kumeneko sadzabwerako. Kodi munthu uyu Koniya ndiye mbiya yopepuka yosweka? Kodi ndiye mbiya yosakondweretsa? Chifukwa chanji atulutsidwa iye, ndi mbeu zake, ndi kuponyedwa m'dziko limene salidziwa? Iwe dziko, dziko, dziko lapansi, tamvera mau a Yehova. Atero Yehova, Lembani munthu uyu wopanda ana, munthu wosaona phindu masiku ake; pakuti palibe munthu wa mbeu zake adzaona phindu, ndi kukhala pa mpando wachifumu wa Davide, ndi kulamuliranso m'Yuda. Tsoka abusa amene athetsa nabalalitsa nkhosa za busa langa! Ati Yehova. Chifukwa chake atero Yehova, Mulungu wa Israele, ponenera abusa amene adyetsa anthu anga: Mwabalalitsa zoweta zanga, ndi kuzipirikitsa, ndipo simunazizonda; taonani, ndidzakusenzani inu kuipa kwa ntchito zanu, ati Yehova. Ndipo ndidzasonkhanitsa zotsala za zoweta zanga za m'maiko onse m'mene ndinazipirikitsiramo, ndipo ndidzazitengeranso kumakola ao; ndipo zidzabalana ndi kuchuluka. Ndipo ndidzaziikira abusa amene adzazidyetsa; sadzaopanso, kapena kutenga nkhawa, sipadzasowa mmodzi yense, ati Yehova. Taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, ndidzamuukitsira Davide Mphukira wolungama, ndipo Iye adzakhala Mfumu, adzachita mwanzeru, nadzachita chiweruzo ndi chilungamo m'dziko lino. Masiku ake Yuda adzapulumutsidwa, ndipo Israele adzakhala mokhazikika, dzina lake adzatchedwa nalo, ndilo Yehova ndiye chilungamo chathu. Chifukwa chake, taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, amene sadzatinso, Pali Yehova, amene anakweza ana a Israele kuwatulutsa m'dziko la Ejipito; koma, Pali Yehova, amene anakweza ndi kutsogolera mbeu za nyumba ya Israele kuwatulutsa m'dziko la kumpoto, ndi kumaiko onse kumene ndinawapirikitsirako, ndipo adzakhala m'dziko lao. Za aneneri. Mtima wanga usweka m'kati mwanga, mafupa anga onse anthunthumira; ndinga munthu woledzera, ngati munthu amene vinyo anamposa; chifukwa cha Yehova, ndi chifukwa cha mau ake opatulika. Pakuti dziko ladzala ndi achigololo; pakuti chifukwa cha temberero dziko lirira, mabusa a kuchipululu auma; kuyenda kwao kuli koipa, ndi mphamvu yao siili yabwino. Pakuti mneneri ndi wansembe onse awiri adetsedwa; inde, m'nyumba yanga ndapeza zoipa zao, ati Yehova. Chifukwa chake njira yao idzakhala kwa iwo yonga malo akuterereka m'mdima; adzachotsedwa, nadzagwa momwemo; pakuti ndidzawatengera zoipa, chaka cha kulangidwa kwao, ati Yehova. Ndipo ndinaona kupusa mwa aneneri a ku Samariya; anenera za Baala, nasocheretsa anthu anga Israele. Mwa aneneri a ku Yerusalemu ndinaona chinthu choopsetsa; achita chigololo, ayenda monama, alimbitsa manja a ochita zoipa, ndipo palibe wobwerera kuleka zoipa zake; onse akhala kwa Ine ngati Sodomu, ndi okhalamo ake ngati Gomora. Chifukwa chake Yehova wa makamu atero za aneneri: Taonani, ndidzadyetsa iwo chowawa, ndidzamwetsa iwo madzi andulu; pakuti kwa aneneri a ku Yerusalemu kuipitsa kwatulukira kunka ku dziko lonse. Yehova wa makamu atero, Musamvere mau a aneneri amene anenera kwa inu; akuphunzitsani zachabe; anena masomphenya a mtima wao, si a m'kamwa mwa Yehova. Anena chinenere kwa iwo akundinyoza Ine, ati Yehova, Mudzakhala ndi mtendere; ndipo kwa yense amene ayenda m'kuumirira kwa mtima wake amati, Palibe choipa chidzagwera inu. Pakuti ndani waima m'upo wa Yehova, kuti aone namve mau ake? Ndani wazindikira mau anga, nawamva? Taonani, chimphepo cha Yehova, kupsa mtima kwake, kwatuluka, inde chimphepo chozungulira; chidzagwa pamutu pa woipa. Mkwiyo wa Yehova sudzabwerera, mpaka atachita, mpaka atatha maganizo a mtima wake; masiku otsiriza mudzachidziwa bwino. Sindinatuma aneneri awa, koma anathamanga; sindinanena ndi iwo, koma ananenera. Koma akadaima m'upo wanga, akadamvetsa anthu anga mau anga, akadatembenuza iwo kunjira yao yoipa, ndi kuchoipa cha ntchito zao. Kodi ndine Mulungu wa pafupi, ati Yehova, si Mulungu wa patali? Kodi munthu angathe kubisala mobisika kuti ndisamuone iye? Ati Yehova. Kodi Ine sindidzala kumwamba ndi dziko lapansi? Ati Yehova. Ndamva chonena aneneri, amene anenera zonama m'dzina langa, kuti, Ndalota, ndalota. Ichi chidzakhala masiku angati m'mtima mwa aneneri amene anenera zonama; ndiwo aneneri a chinyengo cha mtima wao? Amene aganizira kuti adzaiwalitsa anthu anga dzina langa, ndi maloto ao amene anena munthu yense kwa mnansi wake, monga makolo ao anaiwala dzina limene ndimtcha nalo Baala. Mneneri wokhala ndi loto, anene loto lake; ndi iye amene ali ndi mau anga, anene mau anga mokhulupirika. Kodi phesi ndi chiyani polinganiza ndi tirigu? Ati Yehova. Kodi mau anga safanafana ndi moto? Ati Yehova, ndi kufanafana ndi nyundo imene iphwanya mwala? Chifukwa chake, taonani, Ine ndidana ndi aneneri, ati Yehova, amene amaba mau anga, yense kumbera mnansi wake. Taonani, Ine ndidana ndi aneneri, ati Yehova, amene achita ndi malilime ao, ndi kuti, Ati Iye. Taonani, Ine ndidana ndi amene anenera maloto onama, ndi kuwafotokoza ndi kusokeretsa anthu anga ndi zonama zao, ndi matukutuku ao achabe; koma Ine sindinatuma iwo, sindinauza iwo; sadzapindulira konse anthu awa, ati Yehova. Ndipo pamene anthu awa, kapena mneneri, kapena wansembe, adzakufunsa iwe, kuti, Katundu wa Yehova ndi chiyani? Pamenepo uziti kwa iwo, Katundu wanji? Ndidzakuchotsani inu, ati Yehova. Koma za mneneri, ndi wansembe, ndi anthu, amene adzati, Katundu wa Yehova, ndidzamlanga munthuyo ndi nyumba yake. Mudzatero yense kwa mnansi wake, ndi yense kwa mbale wake, Yehova wayankha chiyani? Ndipo Yehova wanena chiyani? Ndipo katundu wa Yehova simudzatchulanso konse; pakuti mau a munthu adzakhala katundu wake; pakuti mwasokoneza mau a Mulungu wamoyo, Yehova wa makamu, Mulungu wathu. Uzitero kwa mneneri, Yehova wakuyankha chiyani? Ndipo Yehova wanenanji? Koma ngati muti, Katundu wa Yehova, chifukwa chake Yehova atero: Chifukwa muti mau awa, Katundu wa Yehova, ndipo ndatuma kwa inu, kuti, Musati, Katundu wa Yehova; chifukwa chake, taonani, ndidzakuiwalani inu konse, ndipo ndidzakuchotsani, ndi mudzi umene ndinakupatsani inu ndi makolo anu, ndidzauchotsa pamaso panga; ndipo ndidzakutengerani inu chitonzo chamuyaya, ndi manyazi amuyaya, amene sadzawailika. Yehova anandionetsa ine, ndipo, taonani, madengu awiri a nkhuyu oikidwa pakhomo pa Kachisi wa Yehova; Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni atachotsa am'nsinga Yekoniya mwana wake wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, ndi akulu a Yuda, ndi amisiri ndi achipala, kuwachotsa ku Yerusalemu, nawatengera ku Babiloni. Dengu limodzi linali ndi nkhuyu zabwinobwino, ngati nkhuyu zoyamba kucha; ndipo dengu limodzi linali ndi nkhuyu zoipaipa, zosadyeka, zinali zoipa. Ndipo Yehova anati kwa ine, Kodi uona chiyani, Yeremiya? Ndipo ndinati, Nkhuyu, nkhuyu zabwino, nzabwino ndithu; zoipazo nzoipa ndithu, zosadyeka poti nzoipa. Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, kuti, Chifukwa Yehova, Mulungu wa Israele, atero, Monga nkhuyu zabwino izi, momwemo ndidzasamalira am'nsinga a Yuda, amene ndawachotsera m'malo muno kunka kudziko la Ababiloni, kuwachitira bwino. Pakuti ndidzaika maso anga pa iwo kuti ndiwachitire iwo bwino, ndipo ndidzawabwezanso kudziko ili: ndipo ndidzamangitsa mudzi wao, osawapasula; ndi kuwabzala, osawazula iwo. Ndipo ndidzapatsa iwo mtima wakundidziwa, kuti ndine Yehova, nadzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao; pakuti adzabwera kwa Ine ndi mtima wao. Ndipo monga nkhuyu zoipa, zosadyeka, poti nzoipa; ntheradi atero Yehova, Chomwecho ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi akulu ake, ndi otsala a m'Yerusalemu, amene atsala m'dziko ili, ndi amene akhala m'dziko la Ejipito. Ndipo ndidzawapatsa akhale choopsetsa choipa ku maufumu a dziko lapansi; akhale chitonzo ndi nkhani ndi choseketsa, ndi chitemberero, monse m'mene ndidzawapirikitsiramo. Ndipo ndidzatuma lupanga, ndi njala, ndi chaola mwa iwo, mpaka athedwa m'dziko limene ndinapatsa iwo ndi makolo ao. Mau amene anadza kwa Yeremiya za anthu onse a Yuda chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda; ndicho chaka choyamba cha Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni; amene mneneri Yeremiya ananena kwa anthu onse a Yuda, ndi onse okhala m'Yerusalemu, kuti: Kuyambira chaka chakhumi ndi chitatu cha Yosiya mwana wake wa Amoni, mfumu ya Yuda, kufikira lero lomwe, zakazi makumi awiri ndi zitatu, mau a Yehova anafika kwa ine, ndipo ndanena kwa inu, pouka mamawa ndi kunena; koma simunamvera. Ndipo Yehova watuma kwa inu atumiki ake onse ndiwo aneneri, pouka mamawa ndi kuwatuma; koma simunamvera, simunatchera khutu lanu kuti mumve; ndi kuti, Mubwerere tsopano nonsenu, yense kuleka njira yake yoipa, ndi zoipa za ntchito zanu, ndi kukhala m'dziko limene Yehova anapatsa inu ndi makolo anu, kuyambira kale kufikira muyaya; musatsate milungu ina kuitumikira, ndi kuigwadira, musautse mkwiyo wanga ndi ntchito ya manja anu; ndingachitire inu choipa. Koma simunandimvera Ine, ati Yehova; kuti muutse mkwiyo wanga ndi ntchito ya manja anu ndi kuonapo choipa inu. Chifukwa chake Yehova wa makamu atero: Popeza simunamvera mau anga, taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo pa dziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya. Ndiponso ndidzawachotsera mau akusekera ndi mau akukondwera, ndi mau a mkwati, ndi mau a mkwatibwi, mau a mphero, ndi kuwala kwa nyali. Ndipo dziko lonseli lidzakhala labwinja, ndi chizizwitso, ndipo mitundu iyi idzatumikira mfumu ya ku Babiloni zaka makumi asanu ndi awiri. Ndipo kudzakhala, zitapita zaka makumi asanu ndi awiri, ndidzalanga mfumu ya ku Babiloni, ndi mtundu uja womwe, ati Yehova, chifukwa cha mphulupulu zao, ndi dziko la Ababiloni; ndipo ndidzaliyesa mabwinja amuyaya. Ndipo ndidzatengera dzikolo mau anga onse amene ndinanenera ilo, mau onse olembedwa m'buku ili, amene Yeremiya wanenera mitundu yonse. Pakuti mitundu yambiri ndi mafumu akulu adzayesa iwo atumiki ao; ndipo ndidzabwezera iwo monga mwa machitidwe ao, monga mwa ntchito ya manja ao. Pakuti Yehova, Mulungu wa Israele, atero kwa ine, Tenga chikho cha vinyo wa ukaliwu pa dzanja langa, ndi kumwetsa mitundu yonse, imene ndikutumizirako. Ndipo adzamwa, nadzayenda dzandidzandi, nadzachita misala, chifukwa cha lupanga limene Ine ndidzatumiza mwa iwo. Ndipo ndinatenga chikho pa dzanja la Yehova, ndinamwetsa mitundu yonse, imene Yehova ananditumizirako; Yerusalemu, ndi midzi ya Yuda, ndi mafumu ake omwe, ndi akulu ake, kuwayesa iwo bwinja, chizizwitso, chotsonyetsa, ndi chitemberero; monga lero lino; Farao mfumu ya ku Ejipito, ndi atumiki ake, ndi akulu ake, ndi anthu ake onse; ndi anthu onse osanganizidwa, ndi mafumu onse a dziko la Uzi, ndi mafumu onse a dziko la Afilisti, ndi Asikeloni, ndi Gaza, ndi Ekeroni, ndi otsala a Asidodi, Edomu, ndi Mowabu, ndi ana a Amoni, ndi mafumu onse a Tiro, ndi mafumu onse a Sidoni, ndi mafumu a chisumbu chimene chili patsidya pa nyanja; Dedani, ndi Tema, ndi Buzi, ndi onse amene ameta m'mbali mwa tsitsi; ndi amfumu onse a Arabiya, ndi mafumu onse a anthu osanganizidwa okhala m'chipululu; ndi mafumu onse a Zimiri, ndi mafumu onse a Elamu, ndi mafumu onse a ku Mediya, ndi mafumu onse a kumpoto, a kutali ndi a kufupi, wina ndi mnzake; ndi maufumu onse a dziko lapansi, okhala pansi pano; ndi mfumu ya Sesaki adzamwa pambuyo pao. Ndipo uziti kwa iwo, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Imwani inu, ndi kuledzera, ndi kusanza, ndi kugwa, osanyamukanso konse, chifukwa cha lupanga limene ndidzatumiza mwa inu. Ndipo padzakhala, ngati akana kutenga chikho pa dzanja lako kuti amwe, uziti kwa iwo, Yehova wa makamu atero: Kumwa muzimwa, Pakuti, taonani, ndiyamba kuchita choipa pa mudzi umene utchedwa ndi dzina langa, kodi inu mudzakhala osalangidwa konse? Simudzakhala osalangidwa; pakuti ndidzaitana lupanga ligwe pa onse okhala m'dziko lapansi, ati Yehova wa makamu. Chifukwa chake muwanenere iwo mau onse awa, ndi kuti kwa iwo, Yehova adzabangula kumwamba, nadzatchula mau ake mokhalamo mwake moyera; adzabangulitsira khola lake; adzafuula, monga iwo akuponda mphesa, adzafuulira onse okhala m'dziko lapansi. Phokoso lidzadza ku malekezero a dziko lapansi; pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi mitundu ya anthu, adzatsutsana ndi anthu onse; koma oipa, adzawapereka kulupanga, ati Yehova. Yehova wa makamu atero, Taonani, zoipa zidzatuluka kumtundu kunka m'mitundu, ndipo namondwe adzauka kuchokera ku malekezero a dziko lapansi. Ndipo akuphedwa a Yehova adzakhala tsiku lomwelo kuchokera ku malekezero ena a dziko lapansi kunka ku malekezero ena a dziko lapansi, sadzaliridwa maliro, sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka. Kuwani, inu abusa, lirani, gubudukani, inu akulu a zoweta; pakuti masiku a kuphedwa kwanu akwanira ndithu, ndipo ndidzakuphwanyani inu, ndipo mudzagwa ngati chotengera chofunika. Ndipo abusa adzasowa pothawira, mkulu wa zoweta adzasowa populumukira. Mau akufuula abusa, ndi kukuwa mkulu wa zoweta! Pakuti Yehova asakaza busa lao. Ndipo makola amtendere adzaonongeka chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Yehova. Wasiya ngaka yake, monga mkango; pakuti dziko lao lasanduka chizizwitso chifukwa cha ukali wa lupanga losautsa, ndi chifukwa cha mkwiyo wake waukali. Poyamba kukhala mfumu Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, panadza mau awa ochokera kwa Yehova, kuti, Yehova atero: Ima m'bwalo la nyumba ya Yehova, ndi kunena kwa midzi yonse ya Yuda, imene imadza kudzagwadira m'nyumba ya Yehova, mau onse amene ndikuuza iwe kuti unene kwa iwo; usasiyepo mau amodzi. Kapena adzamvera, nadzatembenuka, yense kusiya njira yake yoipa; kuti ndileke choipa, chimene ndinati ndiwachitire chifukwa cha kuipa kwa ntchito zao. Ndipo iwe uziti kwa iwo, Yehova atero: Ngati simudzandimvera Ine kuyenda m'chilamulo changa, chimene ndachiika pamaso panu, kumvera mau a atumiki anga aneneri, amene ndituma kwa inu, pouka mamawa ndi kuwatuma iwo, koma simunamvera; pamenepo ndidzayesa nyumba iyi ifanane ndi Silo, ndipo ndidzayesa mudzi uwu chitemberero cha kwa mitundu yonse ya dziko lapansi. Ndipo ansembe ndi aneneri ndi anthu onse anamva Yeremiya alinkunena mau awa m'nyumba ya Yehova. Ndipo panali, pamene Yeremiya anatha kunena mau onse amene Yehova anamuuza iye kuti anene kwa anthu onse, ansembe ndi aneneri ndi anthu onse anamgwira iye, ndi kuti, Udzafa ndithu. Bwanji mwanenera m'dzina la Yehova, kuti, Nyumba iyi idzafanana ndi Silo, mudzi uwu udzakhala bwinja lopanda wokhalamo? Ndipo anthu onse anamsonkhanira Yeremiya m'nyumba ya Yehova. Ndipo pamene akulu a Yuda anamva zimenezi, anakwera kutuluka kunyumba ya mfumu kunka kunyumba ya Yehova; ndipo anakhala pa khomo la chipata chatsopano cha nyumba ya Yehova. Ndipo ansembe ndi aneneri ananena kwa akulu ndi kwa anthu onse, kuti, Munthu uyu ayenera kufa; pakuti wanenera mudzi uwu monga mwamva ndi makutu anu. Pamenepo Yeremiya ananena kwa akulu onse ndi kwa anthu onse, kuti, Yehova anandituma ine ndinenere nyumba iyi ndi mudzi uwu mau onse amene mwamva. Chifukwa chake tsopano konzani njira zanu ndi machitidwe anu, ndi kumvera mau a Yehova Mulungu wanu; ndipo Yehova adzaleka choipa chimene ananenera inu. Koma ine, taonani, ndili m'manja anu; mundichitire ine monga mokomera ndi moyenera m'maso anu. Koma mudziwe ndithu kuti, ngati mudzandipha ine, mudzadzitengera nokha mwazi wosachimwa, ndi pa mudzi uwu, ndi pa okhalamo ake; pakuti mwa ntheradi Yehova wandituma kwa inu kuti ndinene mau onse awa m'makutu anu. Pamenepo akulu ndi anthu onse anati kwa ansembe ndi kwa aneneri, Munthu uyu sayenera kufa: pakuti watinenera ife m'dzina la Yehova Mulungu wathu. Ndipo anauka akulu ena a m'dziko, nati kwa msonkhano wa anthu, kuti, Mika Mmoreseti ananenera masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda; ndipo iye ananena kwa anthu onse a Yuda, kuti, Yehova wa makamu atero: Ziyoni adzalimidwa ngati munda, Yerusalemu adzakhala miunda, ndi phiri la nyumba longa misanje ya nkhalango. Kodi Hezekiya mfumu ya Yuda ndi Yuda wonse anamupha iye konse? Kodi sanamuope Yehova, napembedzera Yehova, ndipo Yehova analeka choipa chimene ananenera iwo? Chotero tidzaichitira miyoyo yathu choipa chachikulu. Ndipo panalinso munthu amene ananenera m'dzina la Yehova, Uriya mwana wake wa Semaya wa ku Kiriyati-Yearimu; ndipo iye ananenera mudzi uwu ndi dziko lino monga mwa mau onse a Yeremiya; ndipo pamene Yehoyakimu mfumu, ndi amphamvu ake onse, ndi akulu onse, anamva mau ake, mfumu inafuna kumupha iye; koma pamene Uriya anamva, anaopa, nathawa, nanka ku Ejipito; ndipo Yehoyakimu mfumu anatuma anthu ku Ejipito, Elinatani mwana wake wa Akibori, ndi anthu ena pamodzi ndi iye, anke ku Ejipito; ndipo anamtulutsa Uriya m'Ejipito, nanka naye kwa Yehoyakimu mfumu; amene anamupha ndi lupanga, naponya mtembo wake m'manda a anthu achabe. Koma dzanja la Ahikamu mwana wa Safani linali ndi Yeremiya, kuti asampereke m'manja a anthu kuti amuphe. Poyamba kukhala mfumu Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, mau awa anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, kuti, Yehova atero kwa ine: Udzipangire zomangira ndi magoli, nuziike pakhosi pako; nuzitumize kwa mfumu ya Edomu, ndi kwa mfumu ya Mowabu, ndi kwa mfumu ya ana a Amoni, ndi kwa mfumu ya Tiro, ndi kwa mfumu ya Sidoni, ndi dzanja la amithenga amene afika ku Yerusalemu kwa Zedekiya mfumu ya Yuda; nuwauze iwo anene kwa ambuyao, kuti, Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero: Muzitero kwa ambuyanu: Ine ndinalenga dziko lapansi, anthu ndi nyama zokhala m'dzikomo, ndi mphamvu yanga yaikulu ndi mkono wanga wotambasuka; ndipo ndinapereka ilo kwa iye amene ayenera pamaso panga. Tsopano ndapereka maiko onse awa m'manja a Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga; ndiponso nyama za kuthengo ndampatsa iye kuti zimtumikire. Ndipo amitundu onse adzamtumikira iye, ndi mwana wake, ndi mdzukulu wake, mpaka yafika nthawi ya dziko lake; ndipo amitundu ambiri ndi mafumu akulu adzamuyesa iye mtumiki wao. Ndipo padzakhala, kuti mtundu ndi ufumu umene sudzamtumikira Nebukadinezara yemweyo mfumu ya ku Babiloni, mtundu umenewo Ine ndidzalanga, ati Yehova, ndi lupanga, ndi njala, ndi chaola, mpaka nditatha onse ndi dzanja lake. Koma inu, musamvere aneneri anu, kapena akuombeza anu, kapena maloto anu, kapena alauli anu, kapena obwebweta anu, Musadzatumikira mfumu ya ku Babiloni; kakuti iwo akunenerani inu zonama, kuti akuchotseni inu m'dziko lanu, kunka kutali kuti ndikupirikitseni inu, ndipo inu mudzathedwa. Koma mtundu umene udzaika khosi lao pansi pa goli la mfumu ya ku Babiloni, ndi kumtumikira iye, mtundu umene ndidzaulola ukhalebe m'dziko lao, ati Yehova; ndipo adzalilima, nadzakhala momwemo. Ndipo ndinanena kwa Zedekiya mfumu ya Yuda monga mau onse amenewa, kuti, Longani makosi anu m'goli la mfumu ya ku Babiloni, ndi kumtumikira iye ndi anthu ake, ndipo mudzakhala ndi moyo. Mudzaferanji, iwe ndi anthu anu, ndi lupanga ndi njala, ndi chaola, monga wanena Yehova za mtundu umene ukana kumtumikira mfumu ya ku Babiloni? Musamvere mau a aneneri amene anena ndi inu, kuti, simudzamtumikira mfumu ya ku Babiloni; pakuti akunenerani zonama. Pakuti sindinawauma iwo, ati Yehova, koma anenera zonama m'dzina langa; kuti ndikupirikitseni inu, kuti mudzathedwe, inu, ndi aneneri amene anenera kwa inu. Ndiponso ndinanena kwa ansembe ndi kwa anthu onsewa, kuti, Yehova atero: Musamvere mau a aneneri anu amene akunenerani inu, kuti, Taonani, zipangizo za nyumba ya Yehova zidzatengedwanso ku Babiloni posachedwa; pakuti akunenerani inu zonama. Musamvere amenewa; mtumikireni mfumu ya ku Babiloni, ndipo mudzakhala ndi moyo; chifukwa chanji mudzi uwu udzakhala bwinja? Koma ngati ndiwo aneneri, ndipo ngati mau a Yehova ali ndi iwo, tsopano apembedzere Yehova wa makamu, kuti zipangizo zotsala m'nyumba ya Yehova, ndi m'nyumba ya mfumu ya Yuda, ndi ku Yerusalemu, zisanke ku Babiloni. Pakuti Yehova wa makamu atero, za zoimiritsa, ndi za thawale, ndi za zoikirapo, ndi za zipangizo zotsala m'mudzi uwu, zimene sanazitenge Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, pamene anamtenga ndende Yekoniya mwana wake wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Babiloni; ndi akulu onse a Yuda ndi Yerusalemu; inde, atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, za zipangizo zotsala m'nyumba ya Yehova, ndi m'nyumba ya mfumu ya Yuda, ndi ku Yerusalemu; adzanka nazo ku Babiloni, kumeneko zidzakhala, mpaka tsiku limene ndidzayang'anira iwo, ati Yehova; pamenepo ndidzazikweza, ndi kuzibwezera kumalo kuno. Ndipo panali chaka chomwecho, poyamba Zedekiya kukhala mfumu ya Yuda, chaka chachinai, mwezi wachisanu, kuti Hananiya mwana wa Azuri mneneri, amene anali wa ku Gibiyoni, ananena ndi ine m'nyumba ya Yehova, pamaso pa ansembe ndi pa anthu onse, kuti, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, kuti, Ndathyola goli la mfumu ya ku Babiloni. Zisanapite zaka ziwiri zamphumphu Ine ndidzabwezeranso kumalo kuno zipangizo zonse za m'nyumba ya Yehova, zimene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anazichotsa muno, kunka nazo ku Babiloni; ndipo ndidzabweranso kumalo kuno Yekoniya mwana wake wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, ndi am'nsinga onse a Yuda, amene ananka ku Babiloni, ati Yehova: pakuti ndidzathyola goli la mfumu ya ku Babiloni. Ndipo Yeremiya mneneri anati kwa Hananiya mneneri pamaso pa ansembe, ndi pamaso pa anthu onse amene anaima m'nyumba ya Yehova, Yeremiya mneneri anati, Amen: Yehova achite chotero: Yehova atsimikize mau ako amene wanenera, abwezerenso zipangizo za nyumba ya Yehova, ndi onse amene anachotsedwa am'nsinga, kuchokera ku Babiloni kudza kumalo kuno. Koma mumvetu mau awa amene ndinena m'makutu anu, ndi m'makutu a anthu onse: Aneneri amene analipo kale ndisanakhale ine, nimusanakhale inu, ananenera maiko ambiri, ndi mafumu akulu, za nkhondo, ndi za choipa, ndi za chaola. Mneneri amene anenera za mtendere, pamene mau a mneneri adzachitidwa, pamenepo mneneri adzadziwika, kuti Yehova anamtuma ndithu. Pamenepo mneneri Hananiya anachotsa goli pa khosi la Yeremiya, nalithyola. Ndipo Hananiya ananena pamaso pa anthu onse, kuti, Yehova atero: Chomwecho ndidzathyola goli la Nebukadinezara mfumu ya Babiloni zisanapite zaka ziwiri zamphumphu kulichotsa pa khosi la amitundu onse. Ndipo Yeremiya mneneri anachoka. Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, atathyola Hananiya mneneri goli kulichotsa pa khosi la Yeremiya, kuti, Pita, nunene kwa Hananiya, kuti Yehova atero: Wathyola magoli amtengo; koma udzapanga m'malo mwao magoli achitsulo. Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Ndaika goli lachitsulo pa khosi la amitundu onsewa, kuti amtumikire Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni; ndipo adzamtumikira iye; ndipo ndampatsanso nyama za kuthengo. Ndipo Yeremiya mneneri ananena kwa Hananiya mneneri, Tamvatu, Hananiya; Yehova sanakutume iwe; koma ukhulupiritsa anthu awa zonama. Chifukwa chake Yehova atero, Taona, Ine ndidzakuchotsa iwe kudziko; chaka chino udzafa, pakuti wanena zopikisana ndi Yehova. Ndipo anafa Hananiya mneneri chaka chomwecho mwezi wachisanu ndi chiwiri. Amenewa ndi mau a kalata uja anatumiza Yeremiya mneneri kuchokera ku Yerusalemu kunka kwa akulu otsala a m'nsinga, ndi kwa ansembe, ndi kwa aneneri, ndi kwa anthu onse, amene Nebukadinezara anawatenga ndende ku Yerusalemu kunka ku Babiloni; anatero atachoka ku Yerusalemu Yekoniya mfumu ndi amake a mfumu ndi adindo ndi akulu a Yuda ndi a ku Yerusalemu, ndi amisiri, ndi achipala, anatumiza kalatayo m'dzanja la Elasa mwana wake wa Safani, ndi Gemariya mwana wake wa Hilikiya, amene Zedekiya mfumu ya Yuda anawatuma ku Babiloni kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, kuti, Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero, kwa am'nsinga onse, amene ndinawatenga ndende ku Yerusalemu kunka nao ku Babiloni: Mangani nyumba, khalani m'menemo; limani minda, idyani zipatso zake; tengani akazi, balani ana aamuna ndi aakazi; kwatitsani ana anu amuna, patsani ananu akazi kwa amuna, kuti abale ana aamuna ndi aakazi; kuti mubalane pamenepo musachepe. Nimufune mtendere wa mudzi umene ndinakutengerani am'nsinga, nimuwapempherere kwa Yehova; pakuti mwa mtendere wake inunso mudzakhala ndi mtendere. Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero: Aneneri anu ndi akuombeza anu amene akhala pakati panu, asakunyengeni inu, musamvere maloto anu amene mulotetsa. Pakuti anenera kwa inu zonama m'dzina langa; sindinatuma iwo, ati Yehova. Pakuti Yehova atero, kuti, Zitapita zaka makumi asanu ndi awiri pa Babiloni, ndidzakuyang'anirani inu, ndipo ndidzakuchitirani inu mau anga abwino, ndi kubwezera inu kumalo kuno. Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a choipa, akukupatsani inu adzukulu ndi chiyembekezero. Pamenepo mudzandiitana Ine, ndipo mudzanka ndi kupemphera kwa Ine, ndipo ndidzakumverani inu. Ndipo mudzandifuna Ine, ndi kundipeza, pamene mundifuna ndi mtima wanu wonse. Ndipo ndidzapezedwa ndi inu, ati Yehova, ndidzabwezanso undende wanu, ndipo ndidzasonkhanitsa inu kwa mitundu yonse, ndi kumalo konse kumene ndinakupirikitsirani inu, ati Yehova; ndipo ndidzakubwezeraninso kumalo kumene ndinakutengani inu andende. Pakuti mwati, Yehova watiutsira ife aneneri m'Babiloni. Pakuti Yehova atero za mfumu imene ikhala pa mpando wachifumu wa Davide, ndi za anthu onse amene akhala m'mudzi uno, abale anu amene sanatulukire pamodzi ndi inu kundende; Yehova wa makamu atero: Taonani, ndidzatuma pa iwo lupanga, ndi njala, ndi chaola, ndipo ndidzayesa iwo onga nkhuyu zoola, zosadyeka, pokhala nzoipa. Ndipo ndidzatsata iwe ndi lupanga, ndi njala, ndi chaola, ndipo ndidzawapereka akhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko la pansi, akhale chitemberero, ndi chodabwitsa, ndi chotsonyetsa, ndi chitonzo, kwa mitundu yonse kumene ndinawapirikitsirako; chifukwa sanamvere mau anga, ati Yehova, amene ndinawatumizira ndi atumiki anga aneneri, ndi kuuka mamawa ndi kuwatuma, koma munakana kumva, ati Yehova. Pamenepo tamvani inu mau a Yehova, inu nonse a m'ndende, amene ndachotsa m'Yerusalemu kunka ku Babiloni. Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, za Ahabu mwana wake wa Koliya, ndi za Zedekiya mwana wake wa Maaseiya, amene anenera zonama m'dzina langa: Taonani, Ndidzawapereka m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni; ndipo iye adzawapha pamaso panu; ndipo am'nsinga onse a Yuda amene ali m'Babiloni adzatemberera pali iwo, kuti, Yehova akuchitire iwe monga Zedekiya ndi Ahabu, amene mfumu ya ku Babiloni inaocha m'moto; chifukwa anachita zopusa m'Israele, nachita chigololo ndi akazi a anansi ao, nanena mau onama m'dzina langa, amene ndinawauza kuti asanene; Ine ndine wodziwa, ndi mboni, ati Yehova. Ndipo za Semaya Mnehelamu uzinena, kuti, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, kuti, Chifukwa watumiza akalata m'dzina lako iwe mwini kwa anthu onse amene akhala ku Yerusalemu, ndi kwa Zefaniya mwana wake wa Maaseiya wansembe, ndi kwa ansembe onse, kuti, Yehova anakuyesa iwe wansembe m'malo mwa Yehoyada wansembe, kuti iwe ndi anzako mudzakhale akapitao m'nyumba ya Yehova, oyang'anira munthu yense wamisala, wodziyesa mneneri, kuti umuike iye m'zigologolo ndi m'goli. Ndipo tsopano, walekeranji kumdzudzula Yeremiya wa ku Anatoti, amene amadziyesa mneneri wanu, popeza watitumizira mau ku Babiloni, akuti, Undende udzakhalitsa; mangani nyumba, khalani m'menemo; limani minda, idyani zipatso zao? Ndipo Zefaniya wansembe anawerenga kalata amene m'makutu a Yeremiya mneneri. Ndipo anadza mau a Yehova kwa Yeremiya, akuti, Uwatumizire mau am'nsinga onse, akuti, Atero Yehova za Semaya Mnehelamu: Chifukwa Semaya wanenera kwa inu, koma Ine sindinamtuma, ndipo anakukhulupiritsani zonama; chifukwa chake atero Yehova, Taonani, ndidzalanga Semaya Mnehelamu, ndi mbeu zake; sadzakhala ndi munthu wakukhala mwa anthu awa, sadzaona zabwino ndidzachitira anthu anga, ati Yehova: chifukwa wanena zopikisana ndi Yehova. Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, kuti, Atero Yehova, Mulungu wa Israele, kuti, Lemba m'buku mau onse amene ndanena kwa iwe. Pakuti, taona, masiku adzadza, ati Yehova, amene ndidzabwezanso undende wa anthu anga Aisraele ndi Ayuda, ati Yehova; ndipo ndidzawabwezera kudziko limene ndinapatsa makolo ao. Ndipo adzakhala nalo. Awa ndi mau ananena Yehova za Israele ndi Yuda. Pakuti Yehova atero: Tamva ife mau akunthunthumira, ndi amantha, si amtendere. Funsani tsopano, ndi kuona ngati mwamuna aona mwana; chifukwa chanji ndiona mwamuna ndi manja ake pa chuuno chake, monga mkazi alinkubala, ndi nkhope zao zotumbuluka? Kalanga ine! Pakuti nlalikulu tsikulo, palibe lina lotere; ndi nthawi ya msauko wa Yakobo; koma adzapulumuka m'menemo. Pakuti padzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, kuti ndidzathyola goli lake pakhosi pako, ndipo ndidzadula zomangira zako; ndipo alendo sadzamuyesanso iye mtumiki wao; koma adzamtumikira Yehova Mulungu wao, ndi Davide mfumu yao, imene Ndidzawaukitsira. Ndipo usaope, iwe Yakobo mtumiki wanga, ati Yehova; usaope, iwe Israele; pakuti, taona, ndidzakupulumutsa iwe kutali, ndi mbeu zako kudziko la undende wao; ndipo Yakobo adzabwera, nadzakhala ndi mtendere, ndipo adzakhala chete, palibe amene adzamuopsa. Pakuti Ine ndili ndi iwe, ati Yehova, kuti ndipulumutse iwe; koma ndidzatha ndithu amitundu onse amene ndinakumwazira mwa iwo, koma sindidzatha iwe ndithu; koma ndidzakulangiza iwe ndi chiweruziro, ndipo sindidzakuyesa wosapalamula. Pakuti atero Yehova, Kulaswa kwako kuli kosapoleka ndi bala lako lili lowawa. Palibe amene adzanenera mlandu wako, ulibe mankhwala akumanga nao bala lako. Mabwenzi ako onse anakuiwala iwe; salikukufuna iwe; pakuti ndakulasa ndi bala la mdani, ndi kulanga kwa wankhanza; chifukwa cha mphulupulu yako yaikulu, chifukwa zochimwa zako zinachuluka. Chifukwa chanji ulirira bala lako? Kuphwetekwa kwako kuli kosapoleka; chifukwa cha mphulupulu yako yaikulu, chifukwa zochimwa zako zinachuluka, ndakuchitira iwe izi. Chifukwa chake iwo akulusira iwe adzalusidwanso; ndi adani ako onse, adzanka ku undende onsewo; ndipo iwo adzakufunkha iwe adzakhala chofunkha, ndipo onse akulanda iwe ndidzapereka kuti zilandidwe zao. Pakuti ndidzakubwezera iwe moyo, ndipo ndidzapoletsa mabala ako, ati Yehova; chifukwa anatcha iwe wopirikitsidwa, nati, Ndiye Ziyoni, amene kulibe munthu amfuna. Atero Yehova: Taonani, ndidzabwezanso undende wa mahema a Yakobo, ndipo ndidzachitira chifundo zokhalamo zake, ndipo mudzi udzamangidwa pamuunda pake, ndi chinyumba chidzakhala momwe. Ndipo padzatuluka pa izo mayamikiro ndi mau a iwo okondwerera; ndipo ndidzachulukitsa iwo, sadzakhala owerengeka; ndidzawachitiranso ulemu, sadzachepa. Ana aonso adzakhala monga kale, ndipo msonkhano wao udzakhazikika pamaso panga, ndipo ndidzalanga onse amene akupsinja iwo. Ndipo mkulu wao adzakhala mwa iwo, ndi wolamulira wao adzatuluka pakati pao; ndipo ndidzamyandikitsa iye, ndipo adzayandikira kwa Ine, pakuti iye wolimba mtima kuyandikira kwa Ine ndani? Ati Yehova. Ndipo inu mudzakhala anthu anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu. Taonani, chimphepo cha Yehova, kupsa mtima kwake, chatuluka, chimphepo chakukokolola: chidzagwa pamtu pa oipa. Mkwiyo waukali wa Yehova sudzabwerera, mpaka wachita, mpaka watha zomwe afuna kuchita m'mtima mwake: masiku akumaliza mudzachizindikira. Nthawi yomweyo, ati Yehova, ndidzakhala Mulungu wa mabanja onse a Israele, ndipo iwo adzakhala anthu anga. Atero Yehova, Anthu opulumuka m'lupanga anapeza chisomo m'chipululu; Israele, muja anakapuma. Yehova anaonekera kwa ine kale, ndi kuti, Inde, ndakukonda iwe ndi chikondi chosatha; chifukwa chake ndakukoka iwe ndi kukukomera mtima. Ndidzamangitsanso mudzi wako, ndipo udzamangidwa, iwe namwali wa Israele; udzakometsedwanso ndi mangaka, ndipo udzatulukira masewero a iwo akukondwerera. Ndiponso udzalima minda ya mphesa pa mapiri a Samariya; akuoka adzaoka, nadzayesa zipatso zake zosapatulidwa. Pakuti lidzafika tsiku, limene alonda a pa mapiri a Efuremu adzafuula, Ukani inu, tikwere ku Ziyoni kwa Yehova Mulungu wathu. Pakuti Yehova atero, Imbirani Yakobo ndi kukondwa, fuulirani mtundu woposawo; lalikirani, yamikirani, ndi kuti, Yehova, mupulumutse anthu anu, ndi otsala a Israele. Taonani, ndidzatenga iwo kudziko la kumpoto, ndidzasonkhanitsa iwo ku malekezero a dziko lapansi, pamodzi ndi osaona ndi opunduka mwendo, mkazi amene ali ndi pakati ndi mkazi alinkubala pamodzi; khamu lalikulu lidzabwera kuno. Adzadza ndi kulira, ndipo ndidzawatsogolera ndi mapembedzero, ndidzawayendetsa kumitsinje yamadzi, m'njira yoongoka m'mene sadzaphunthwa, pakuti ndili Atate wake wa Israele, ndipo Efuremu ali mwana wanga woyamba. Tamvani mau a Yehova, amitundu inu, lalikirani m'zisumbu zakutali; ndi kuti, Iye amene anabalalitsa Israele adzasonkhanitsa, nadzamsunga, monga mbusa achita ndi zoweta zake. Pakuti Yehova wapulumutsa Yakobo, namuombola iye m'dzanja la iye amene anamposa mphamvu. Ndipo adzadza nadzaimba pa msanje wa Ziyoni, nadzasonkhanira ku zokoma za Yehova, kutirigu, ndi kuvinyo, ndi mafuta, ndi kwa ana a zoweta zazing'ono ndi zazikulu; ndipo moyo wao udzakhala ngati munda wamichera; ndipo sadzakhalanso konse ndi chisoni. Ndipo namwali adzasangalala m'masewero, ndi anyamata ndi nkhalamba pamodzi; pakuti ndidzasandutsa kulira kwao kukhale kukondwera, ndipo ndidzatonthoza mitima yao, ndi kuwasangalatsa iwo asiye chisoni chao. Ndipo ndikhutitsa moyo wa ansembe ndi mafuta, ndipo anthu anga adzakhuta ndi zokoma zanga, ati Yehova. Atero Yehova: Mau a amveka m'Rama, maliro ndi kulira kwakuwawa, Rakele alinkulirira ana ake; akana kutonthozedwa mtima pa ana ake, chifukwa palibe iwo. Yehova atero: Letsa mau ako asalire, ndi maso anu asagwe misozi; pakuti ntchito yako idzalandira mphotho, ati Yehova; ndipo adzabweranso kuchokera kudziko la mdani. Ndipo chilipo chiyembekezero cha chitsirizo chako, ati Yehova; ndipo ana ako adzafikanso ku malire ao. Kumva ndamva Efuremu alinkulirira kotero, Mwandilanga ine, ndipo ndalangidwa, monga mwanawang'ombe wosazolowera goli; munditembenuze ine, ndipo ine ndidzatembenuka; pakuti inu ndinu Yehova Mulungu wanga. Pakuti nditatembenuka, ndinalapa; nditalangizidwa, ndinamenya pa ntchafu yanga; ndinakhala ndi manyazi, inde, ndinapepulidwa, chifukwa ndinasenza chitonzo cha ubwana wanga. Kodi Efuremu ndiye mwana wanga wokondedwa? Kodi ndiye mwana wokondweretsa? Nthawi zonse zoti ndimnenera zomtsutsa, pakuti ndimkumbukiranso ndithu; chifukwa chake mumtima mwanga ndimlirira; ndidzamchitiradi chifundo, ati Yehova. Taimitsa zizindikiro, udzipangire zosonyeza; taika mtima wako kuyang'anira mseu wounda, njira imene unapitamo; tatembenukanso, iwe namwali wa Israele, tatembenukiranso kumidzi yako iyi. Udzayenda kwina ndi kwina masiku angati, iwe mwana wamkazi wobwerera m'mbuyo? Pakuti Yehova walenga chatsopano m'dziko lapansi: mkazi adzasanduka mphongo. Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Kawirinso adzanena mau awa m'dziko la Yuda ndi m'midzi yake, pamene ndibwezanso undende wao; Yehova akudalitse iwe, wokhalamo chilungamo, iwe phiri lopatulika. Ndipo Yuda ndi midzi yake yonse adzakhalamo pamodzi; alimi, ndi okusa zoweta. Pakuti ndakhutidwa mtima wolema, ndadzazanso mtima uliwonse wachisoni. Pamenepo ndinauka, ndinaona; ndipo tulo tanga tinandizunira ine. Taonani, masiku adza, ati Yehova, amene ndidzafesera nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda ndi mbeu ya anthu ndi mbeu ya nyama. Ndipo padzakhala kuti, monga ndayang'anira iwo kuzula ndi kupasula ndi kugwetsa, ndi kuononga ndi kusautsa; momwemo ndidzayang'anira iwo kumangitsa mudzi ndi kubzala, ati Yehova. Masiku omwewo sadzanenanso, Atate adya mphesa zowawa, ndi mano a ana ayayamira. Koma yense adzafa chifukwa cha mphulupulu yake; yense amene adya mphesa zowawa, mano ake adzayayamira. Taonani masiku adza, ati Yehova, ndipo ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya Israele, ndi nyumba ya Yuda; si monga pangano limene ndinapangana ndi makolo ao tsiku lija ndinawagwira manja kuwatulutsa m'dziko la Ejipito; pangano langa limenelo analiswa, ngakhale ndinali mbuyao, ati Yehova. Koma ili ndi pangano limene ndidzapangana ndi nyumba ya Israele atapita masiku aja, ati Yehova; ndidzaika chilamulo changa m'kati mwao, ndipo m'mtima mwao ndidzachilemba; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, nadzakhala iwo anthu anga; ndipo sadzaphunzitsa yense mnansi wake, ndi yense mbale wake, kuti, Mudziwe Yehova; pakuti iwo onse adzandidziwa, kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu wa iwo, ati Yehova; pakuti ndidzakhululukira mphulupulu yao, ndipo sindidzakumbukira tchimo lao. Yehova atero, amene apatsa dzuwa kuti liunikire usana, ndi malemba a mwezi ndi a nyenyezi kuti aunikire usiku, amene atonthoza nyanja, pamene mafunde ake agavira; Yehova wa makamu ndi dzina lake: Ngati malembawa achoka pamaso panga, ati Yehova, pamenepo mbeunso ya Israele idzaleka kukhala mtundu pamaso panga kunthawi zonse. Atero Yehova, Ngati ukhoza kuyesa thambo la kumwamba, ndi kusanthula pansi maziko a dziko, pamenepo ndidzachotsa mbeu zonse za Israele chifukwa cha zonse anazichita, ati Yehova. Taonani, masiku adza, ati Yehova, amene mudziwu udzamangidwira Yehova kuyambira pa nsanja ya Hananele kufikira kuchipata cha kungodya. Ndipo chingwe choyesera chidzatulukanso kulunjika ku chitunda cha Garebu, ndipo chidzazungulira kunka ku Gowa. Ndipo chigwa chonse cha mitembo, ndi cha phulusa, ndi minda yonse kufikira kumtsinje wa Kidroni, kufikira kungodya kwa chipata cha akavalo kuloza kum'mawa, ponsepo padzapatulikira Yehova; sipadzazulidwa, sipadzagwetsedwa konse kunthawi zamuyaya. Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova chaka chakhumi cha Zedekiya mfumu ya Yuda, chimene chinali chaka chakhumi ndi chisanu ndi chitatu cha Nebukadinezara. Nthawi yomweyo nkhondo ya mfumu ya Babiloni inamangira Yerusalemu misasa; ndipo Yeremiya mneneri anatsekeredwa m'bwalo la kaidi, linali kunyumba ya mfumu ya Yuda. Pakuti Zedekiya mfumu ya Yuda inamtsekera iye, nati, Chifukwa chanji ulinkunenera, kuti, Yehova atero, Taonani, ndidzapereka mudzi uwu m'dzanja la mfumu ya Babiloni, ndipo iye adzaulanda, ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda sadzapulumuka m'dzanja la Ababiloni, koma adzaperekedwadi m'dzanja la mfumu ya Babiloni, ndipo adzanena ndi iye pakamwa ndi pakamwa, ndipo adzaonana maso ndi maso; ndipo adzatsogolera Zedekiya kunka ku Babiloni, ndipo adzakhala komwe kufikira ndidzamzonda, ati Yehova: ngakhale mudzamenyana ndi Ababiloni, simudzapindula konse? Ndipo Yeremiya anati, Mau a Yehova anadza kwa ine, kuti, Taonani, Hanamele mwana wa Salumu mbale wa atate wako adzadza kwa iwe, kuti, Ugule munda wanga uli ku Anatoti; pakuti mphamvu yakuombola ndi yako kuugula. Ndipo Hanamele mwana wa mbale wa atate wanga anadza kwa ine m'bwalo la kaidi monga mwa mau a Yehova, nati kwa ine, Gulatu munda wanga, wa ku Anatoti, m'dziko la Benjamini; pakuti mphamvu yakulowa ndi yakuombola ndi yako; udzigulire wekha. Pamenepo ndinadziwa kuti awa ndi mau a Yehova. Ndipo ndinagula mundawo wa ku Anatoti kwa Hanamele mwana wa mbale wa atate wanga, ndimyesera ndalama, masekeli khumi ndi asanu ndi awiri a siliva. Ndipo ndinalemba chikalatacho, ndichisindikiza, ndiitana mboni zambiri, ndiyesa ndalama m'miyeso. Ndipo ndinatenga kalata wogulira, wina wosindikizidwa, monga mwa lamulo ndi mwambo, ndi wina wovundukuka; ndipo ndinapereka kalata wogulirayo kwa Baruki mwana wa Neriya, mwana wa Maseiya, pamaso pa Hanamele mwana wa mbale wa atate wanga, ndi pamaso pa mboni zimene zinalemba pa kalata wogulirayo, pamaso pa Ayuda onse okhala m'bwalo la kaidi. Ndipo ndinauza Baruki pamaso pao, kuti, Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero; Tenga akalata awa, kalata uyu wogulira, wosindikizidwa, ndi kalata uyu wovundukuka, nuwaike m'mbiya yadothi; kuti akhale masiku ambiri. Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero: Nyumba ndi minda ndi minda yamphesa idzagulidwanso m'dziko muno. Ndipo nditapereka kalata wogulirayo kwa Baruki mwana wa Neriya, ndinapemphera kwa Yehova, kuti, Ha! Yehova Mulungu, taonani, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi mphamvu yanu yaikulu ndi mkono wanu wotambasuka; palibe chokanika Inu; amene muchitira chifundo anthu zikwi; nimubwezera mphulupulu ya atate m'chifukwa cha ana ao a pambuyo pao, dzina lake ndi Mulungu wamkulu, wamphamvu, Yehova wa makamu; wamkulu m'upo, wamphamvu m'ntchito; maso anu ali otsegukira njira zonse za ana a anthu; kuti mupatse yense monga mwa chipatso cha machitidwe ake; amene munaika zizindikiro ndi zodabwitsa m'dziko la Ejipito, mpaka lero lomwe, m'Israele ndi mwa anthu ena; nimunadzitengera mbiri, monga lero lomwe; ndipo munatulutsa anthu anu Israele m'dziko la Ejipito ndi zizindikiro, ndi zodabwitsa, ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mantha ambiri; ndipo munawapatsa iwo dziko ili, limene munalumbirira makolo ao kuti mudzawapatsa, dziko moyenda mkaka ndi uchi; ndipo analowa, nakhalamo; koma sanamvere mau anu, sanayende m'chilamulo chanu; sanachite kanthu ka zonse zimene munawauza achite; chifukwa chake mwafikitsa pa iwo choipa chonsechi; taonani mitumbira, yafika kumudzi kuugwira, ndipo mudzi uperekedwa m'dzanja la Ababiloni olimbana nao, chifukwa cha lupanga, ndi chifukwa cha njala, ndi chifukwa cha chaola; ndipo chimene munachinena chaoneka; ndipo, taonani, muchiona. Ndipo Inu Yehova Mulungu mwati kwa ine, Udzigulire munda ndi ndalama, nuitane mboni; koma mudzi waperekedwa m'manja a Ababiloni. Ndipo anadza mau a Yehova kwa Yeremiya, kuti, Taona, Ine ndine Yehova, Mulungu wa anthu onse; kodi kuli kanthu kondilaka Ine? Chifukwa chake Yehova atero: Taona, ndidzapereka mudziwu m'dzanja la Ababiloni, m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzaulanda, ndipo Ababiloni, olimbana ndi mudzi uwu, adzafika nadzayatsa mudziwu, nadzautentha, pamodzi ndi nyumba, zimene anafukizira Baala, pa machitidwe ao, ndi kutsanulirira milungu ina nsembe zothira, kuti autse mkwiyo wanga. Pakuti ana a Israele ndi ana a Yuda anachita zoipa zokhazokha pamaso panga chiyambire ubwana wao, pakuti ana a Israele anandiputa Ine kokhakokha ndi ntchito ya manja ao, ati Yehova. Pakuti mudzi uwu unali woutsa mkwiyo wanga ndi ukali wanga kuyambira tsiku lija anaumanga mpaka lero, kuti ndiuchotse pamaso panga; chifukwa cha zoipa zonse za ana a Israele ndi za ana a Yuda, zimene anandiputa nazo Ine, iwowo, mafumu ao, akulu ao, ansembe ao, aneneri ao, ndi anthu a Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu. Ndipo anandipatsa Ine mbuyo, si nkhope, ngakhale ndinawaphunzitsa, kuuka m'mamawa ndi kuwaphunzitsa, koma sanamvere kulangizidwa. Koma anaika zonyansa zao m'nyumba yotchedwa dzina langa, kuti aidetse. Ndipo anamanga misanje ya Baala, ili m'chigwa cha mwana wake wa Hinomu, kuti apitirize kumoto ana ao aamuna ndi aakazi chifukwa cha Moleki; chimene sindinauza, chimene sichinalowa m'mtima mwanga, kuti achite chonyansa ichi, chochimwitsa Yuda. Chifukwa chake tsopano atero Yehova, Mulungu wa Israele, za mudzi umene, munena inu, waperekedwa m'dzanja la mfumu ya Babiloni ndi lupanga, ndi njala, ndi chaola: Taonani, ndidzawasokolotsa m'maiko monse, kumene ndinawapirikitsira ndi mkwiyo wanga, ndi m'kupsa mtima kwanga, ndi mu ukali waukulu, ndipo ndidzawabwezeranso kumalo kuno, ndipo ndidzawakhazikitsa mokhulupirika, ndipo adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao; ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi ndi njira imodzi, kuti andiope Ine masiku onse; kuwachitira zabwino, ndi ana ao pambuyo pao; ndipo ndidzapangana nao pangano lamuyaya, kuti sindidzawachokera kuleka kuwachitira zabwino; koma ndidzalonga kuopsa kwanga m'mitima yao, kuti asandichokere. Inde, ndidzasekerera iwo kuwachitira zabwino, ndipo ndidzawaoka ndithu m'dziko lino ndi mtima wanga wonse ndi moyo wanga wonse. Pakuti atero Yehova: Monga ndatengera anthu awa choipa chonsechi, chomwecho ndidzatengera iwo zabwino zonse ndawalonjeza. Ndipo minda idzagulidwa m'dziko lino, limene muti, Ndilo bwinja, lopanda munthu kapena nyama; loperekedwa m'dzanja la Ababiloni. Anthu adzagula minda ndi ndalama, adzalembera akalata ogulira, adzawasindikiza, adzaitana mboni, m'dziko la Benjamini, ndi m'malo ozungulira Yerusalemu, ndi m'midzi ya Yuda, ndi m'midzi ya kumtunda, ndi m'midzi ya kuchidikha, ndi m'midzi ya kumwera; pakuti ndidzabweza undende wao, ati Yehova. Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya nthawi yachiwiri, pamene iye anali chitsekedwere m'bwalo la kaidi, kuti, Atero Yehova wochita zake, Yehova wolenga zake kuti azikhazikitse; dzina lake ndi Yehova: Undiitane Ine, ndipo Ine ndidzakuyankha iwe, ndipo ndidzakusonyeza iwe zazikulu, ndi zolakika, zimene suzidziwa. Pakuti atero Yehova, Mulungu wa Israele, za nyumba za mudzi uno, ndi za nyumba za mafumu a Yuda'zi, zinagwetsedwa ziwatchinjirizire mitumbira, ndi lupanga: Adza kumenyana ndi Ababiloni, koma adzangozidzaza ndi mitembo ya anthu, amene ndawapha m'mkwiyo wanga ndi mu ukali wanga, amene ndabisira mudzi uno nkhope yanga chifukwa cha zoipa zao zonse. Taonani, ndidzautengera moyo ndi kuuchiritsa, ndi kuwachiritsa; ndipo ndidzawaululira iwo kuchuluka kwa mtendere ndi zoona. Ndipo ndidzabweza undende wa Yuda ndi wa Israele, ndipo ndidzamangitsa mudzi wao, monga poyamba paja. Ndipo ndidzawayeretsa kuchotsa mphulupulu yao, imene anandichimwira Ine; ndipo ndidzakhululukira mphulupulu zao zimene anandichimwira, nandilakwira Ine. Ndipo ndidzayesa mudzi uno chifukwa cha kukondwa, ndi chiyamiko ndi ulemerero, pamaso pa amitundu onse a pa dziko lapansi, amene adzamva zabwino zonse ndidzawachitirazo, ndipo adzaopa nadzanthunthumira chifukwa cha zabwino zonse ndi mtendere wonse zimene ndidzauchitira. Atero Yehova: M'malo muno, m'mene muti, Ndi bwinja, mopanda munthu, mopanda nyama, m'midzi ya Yuda, m'makwalala a Yerusalemu, amene ali bwinja, opanda munthu, opanda wokhalamo, opanda nyama, mudzamvekanso mau akukondwa ndi mau akusekera, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi, mau a iwo akuti, Myamikireni Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndiye wabwino, chifundo chake nchosatha; ndi a iwo akutengera nsembe zoyamikira m'nyumba ya Yehova. Pakuti ndidzabweza undende wa dziko monga poyamba, ati Yehova. Yehova wa makamu atero: M'malo muno, muli bwinja, mopanda munthu ndi nyama, m'midzi yake yonse, mudzakhalanso mokhalamo abusa ogonetsa zoweta zao. M'midzi ya kumtunda, m'midzi ya kuchidikha, m'midzi ya kumwera, m'dziko la Benjamini, m'malo ozungulira Yerusalemu, m'midzi ya Yuda, zoweta zidzapitanso pansi pa manja a iye amene aziwerenga, ati Yehova. Taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, ndidzakhazikitsa mau abwino aja ndinanena za nyumba ya Israele ndi za nyumba ya Yuda. Masiku aja, nthawi ija, ndidzamphukutsira Davide mphukira ya chilungamo; ndipo adzachita chiweruzo ndi chilungamo m'dzikomu. Masiku omwewo Yuda adzapulumutsidwa, ndi Yerusalemu adzakhala mokhulupirika; ili ndi dzina adzatchedwa nalo, Yehova ndiye chilungamo chathu. Pakuti Yehova atero: Davide sadzasowa munthu wokhala pa mpando wachifumu wa nyumba ya Israele; ndiponso ansembe a fuko la Levi sadzasowa munthu pamaso panga wakupereka nsembe zopsereza, ndi kutentha nsembe zaufa, ndi wakuchita nsembe masiku onse. Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, kuti, Pakuti Yehova atero: Ngati mukhoza kuswa pangano langa la usana ndi pangano langa la usiku, kuti usakhalenso usana ndi usiku, m'nyengo yao; pamenepo pangano langa lidzasweka ndi Davide mtumiki wanga, kuti asakhale ndi mwana wamwamuna wakulamulira pa mpando wa ufumu wake; ndiponso ndi Alevi ansembe, atumiki anga. Monga khamu la kuthambo silingathe kuwerengedwa, ndi mchenga wa kunyanja sungathe kuyesedwa; chomwecho ndidzachulukitsa mbeu za Davide mtumiki wanga, ndi Alevi akunditumikira Ine. Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, kuti, Kodi sulingalira chomwe anena anthu awa, kuti, Mabanja awiri amene Yehova anawasankha, wataya iwo? Chomwecho anyoza anthu anga, kuti asakhalenso mtundu pamaso pao. Yehova atero: Likaleka kukhala pangano langa la usana ndi usiku, ngati sindinalemba malemba a kumwamba ndi dziko lapansi; pamenepo ndidzatayanso mbeu ya Yakobo, ndi ya Davide mtumiki wanga, kuti sindidzatenganso za mbeu zake kuti zikhale zolamulira mbeu za Abrahamu, ndi za Isaki, ndi za Yakobo; pakuti ndidzabweza undende wao, ndipo ndidzawachitira chifundo. Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, pamene Nebukadinezara mfumu ya Babiloni, ndi nkhondo yake yonse, ndi maufumu onse a dziko lapansi amene anagwira mwendo wake, ndi anthu onse, anamenyana ndi Yerusalemu, ndi midzi yake yonse, akuti: Yehova Mulungu wa Israele atero, Pita, nena kwa Zedekiya mfumu ya Yuda, numuuze iye, kuti Yehova atero, Taona, ndidzapereka mudziwu m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo adzautentha ndi moto; ndipo iwe sudzapulumuka m'dzanja lake, koma udzagwiridwadi, nudzaperekedwa m'dzanja lake; ndipo maso ako adzaonana nao a mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzanena nawe pakamwa ndi pakamwa, ndipo udzanka ku Babiloni. Koma tamva mau a Yehova, iwe Zedekiya mfumu ya Yuda; Yehova atero za iwe, Sudzafa ndi lupanga; udzafa ndi mtendere; ndipo adzawambika iwe monga anawambika makolo ako, mafumu akale usanakhale iwe; ndipo adzakulirira iwe, kuti, Kalanga ine ambuye! Pakuti ndanena mau, ati Yehova. Ndipo Yeremiya mneneri ananena mau onsewa kwa Zedekiya mfumu ya Yuda m'Yerusalemu, pamene nkhondo ya mfumu ya ku Babiloni inamenyana ndi Yerusalemu, ndi midzi yonse ya Yuda imene inatsala, ndi Lakisi ndi Azeka; pakuti midzi ya Yuda yamalinga yotsala ndi imeneyi. Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, mfumu Zedekiya atapangana pangano ndi anthu onse amene anali pa Yerusalemu, kuti awalalikire iwo ufulu; kuti yense ammasule kapolo wake wamwamuna, ndi wamkazi, pokhala iye Muhebri wamwamuna kapena wamkazi, kuti yense asayese Myuda mnzake kapolo wake; ndipo akulu onse ndi anthu onse anamvera, amene anapangana mapangano, akuti yense ammasule kapolo wake wamwamuna, kapena wamkazi osawayesanso akapolo; iwo anamvera nawamasula; koma pambuyo pake anabwerera, nabweza akapolo ake aamuna ndi aakazi, amene anawamasula, nawagonjetsanso akhale akapolo aamuna ndi aakazi; chifukwa chake mau a Yehova anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, kuti, Yehova Mulungu wa Israele atero: Ndinapangana mapangano ndi makolo anu tsiku lija ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito, kutuluka m'nyumba ya ukapolo, kuti, Zitapita zaka zisanu ndi ziwiri mudzaleka amuke yense mbale wake amene ali Muhebri, amene anagulidwa ndi inu, amene anakutumikirani inu zaka zisanu ndi chimodzi, mudzammasule akuchokereni; koma makolo anu sanandimvere Ine, sananditchere Ine khutu. Ndipo mwabwerera inu tsopano, ndi kuchita chimene chili cholungama pamaso panga, pakulalikira ufulu yense kwa mnzake; ndipo munapangana pangano pamaso panga m'nyumba imene itchedwa dzina langa; koma mwabwerera ndi kuipitsa dzina langa, ndi kubwezera m'ukapolo yense kapolo wake wamwamuna, ndi wamkazi, amene munammasula akachite zao, ndipo munawagonjetsa, akhale akapolo anu aamuna ndi aakazi. Chifukwa chake Yehova atero: Simunandimvera Ine, kuti mulalikire ufulu, munthu yense kwa mbale wake, ndi munthu yense kwa mnzake; taonani, ndilalikira kwa inu ufulu, ati Yehova, wa kulupanga, kuchaola, ndi kunjala; ndipo ndidzakuperekani mukhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko lapansi. Ndipo ndidzapereka anthu akulakwira pangano langa, amene sanachite mau a pangano limene anapangana pamaso panga, muja anadula pakati mwanawang'ombe ndi kupita pakati pa mbali zake; akulu a Yuda, ndi akulu a Yerusalemu, adindo, ndi ansembe, ndi anthu onse a m'dziko, amene anapita pakati pa mbali za mwanawang'ombe; ndidzapereka iwo m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la iwo akufuna moyo wao; ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame za mlengalenga, ndi cha zilombo za pa dziko lapansi. Ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda ndi akulu ake ndidzawapereka m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la akufuna moyo wao, ndi m'dzanja la nkhondo ya mfumu ya ku Babiloni, imene yakuchokereani. Taonani, ndidzauza, ati Yehova, ndidzabwezera iwo kumudzi uno; ndipo adzamenyana nao, nadzaulanda, nadzautentha ndi moto; ndipo ndidzayesa midzi ya Yuda mabwinja, palibenso wokhalamo. Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova masiku a Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, kuti, Pita kunyumba ya Arekabu, nunene nao, nulowetse iwo m'nyumba ya Yehova, m'chipinda china, nuwapatse iwo vinyo amwe. Ndipo ndinatenga Yazaniya mwana wa Yeremiya, mwana wa Habaziniya, ndi abale ake, ndi ana amuna ake, ndi nyumba yonse ya Arekabu; ndipo ndinawalowetsa m'nyumba ya Yehova, m'chipinda cha ana a Hanani mwana wa Igadaliya, munthu wa Mulungu, chokhala pambali pa chipinda cha akulu, ndicho chosanjika pa chipinda cha Maaseiya mwana wa Salumu, mdindo wa pakhomo; ndipo ndinaika pamaso pa ana amuna a nyumba ya Arekabu mbale zodzala ndi vinyo, ndi zikho, ndipo ndinati kwa iwo, Imwani vinyo. Koma anati, Sitidzamwa vinyo; pakuti Yonadabu mwana wa Rekabu kholo lathu anatiuza ife, kuti, Musadzamwe vinyo, kapena inu, kapena ana anu, kumuyaya; ndiponso musamange nyumba, musafese mbeu, musaoke mipesa, musakhale nayo; koma masiku anu onse mudzakhale m'mahema; kuti mukhale ndi moyo masiku ambiri m'dziko limene mukhalamo alendo. Ndipo ife tamva mau a Yonadabu mwana wa Rekabu kholo lathu m'zonse zimene anatiuza ife, zakuti tisamwe vinyo masiku athu onse, ife, akazi athu, ana athu aamuna ndi aakazi; ngakhale kudzimangira nyumba zokhalamo; ndipo sitili nao munda wamphesa, kapena munda, kapena mbeu; koma takhala m'mahema, ntimvera, ntichita monga mwa zonse anatiuza Yonadabu kholo lathu. Koma panali, pamene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anadza m'dzikomu, ife tinati, Tiyeni tinke ku Yerusalemu chifukwa tiopa nkhondo ya Ababiloni, ndi nkhondo ya Aramu; ndipo tikhala m'Yerusalemu. Ndipo anadza mau a Yehova kwa Yeremiya, kuti, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Pita, nunene kwa anthu a Yuda ndi kwa okhala m'Yerusalemu, Kodi simudzalola kulangizidwa kumvera mau anga? Ati Yehova. Mau a Yonadabu mwana wa Rekabu, amene anauza ana ake, asamwe vinyo, alikuchitidwa, ndipo mpaka lero samamwa, pakuti amvera lamulo la kholo lao; koma Ine ndanena ndi inu, ndalawirira ndi kunena; koma simunandimvera Ine. Ndatumanso kwa inu atumiki anga onse aneneri, ndalawirira ndi kuwatuma, kuti, Bwererani kuleka yense njira yake yoipa, konzani machitidwe anu, musatsate milungu ina kuitumikira, ndipo mudzakhala m'dziko limene ndakupatsani inu ndi makolo anu; koma simunanditchera khutu lanu, simunandimvera Ine. Pakuti monga ana a Yonadabu mwana wa Rekabu achita lamulo la kholo lao limene anawauza, koma anthu awa sanandimvere Ine. Chifukwa chake atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele: Taonani, ndidzafikitsa pa Yuda ndi pa onse okhala m'Yerusalemu choipa chonsecho ndawanenera iwo; chifukwa ndanena ndi iwo, koma sanamve; ndaitana, koma iwo sanandivomere. Ndipo Yeremiya anati kwa nyumba ya Arekabu, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Chifukwa mwamvera lamulo la Yonadabu kholo lanu, ndi kusunga zonse anakulangizani inu, ndi kuchita monga mwa zonse anakuuzani inu; chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Yonadabu mwana wa Rekabu sadzasowa munthu wakuima pamaso panga kumuyaya. Ndipo panali chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, mau awa anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, kuti, Tenga buku lampukutu, nulembe m'menemo mau onse ndanena kwa iwe akunenera Israele, ndi akunenera Yuda, ndi akunenera amitundu onse kuyambira tsiku ndinanena kwa iwe, kuyambira masiku a Yosiya, mpaka lero. Kapena nyumba ya Yuda idzamva choipa chonse chimene nditi ndidzawachitire; kuti abwerere yense kuleka njira yake yoipa; kuti ndikhululukire mphulupulu yao ndi tchimo lao. Ndipo Yeremiya anaitana Baruki mwana wa Neriya; ndipo Yeremiya analembetsa Baruki m'buku lampukutu mau onse a Yehova, amene ananena naye. Ndipo Yeremiya anauza Baruki, kuti, Ndaletsedwa sindithai kulowa m'nyumba ya Yehova; koma pita iwe, nuwerenge mu mpukutu umene ndakulembetsa, mau a Yehova m'makutu a anthu m'nyumba ya Yehova tsiku lakusala kudya; ndiponso udzawawerenga m'makutu a Ayuda onse amene atuluka m'midzi yao. Kapena pembedzero lao lidzagwa pamaso pa Yehova, ndipo adzabwerera yense kuleka njira yake yoipa; pakuti mkwiyo ndi ukali umene Yehova wanenera anthu awa ndi waukulu. Ndipo Baruki mwana wa Neriya anachita monga mwa zonse anamuuza iye Yeremiya mneneri, nawerenga m'buku mau a Yehova m'nyumba ya Yehova. Ndipo panali chaka chachisanu cha Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, mwezi wachisanu ndi chinai, anthu onse a m'Yerusalemu, ndi anthu onse ochokera m'midzi ya Yuda kudza ku Yerusalemu, analalikira kusala kudya pamaso pa Yehova. Ndipo Baruki anawerenga m'buku mau a Yeremiya m'nyumba ya Yehova, m'chipinda cha Gemariya mwana wa Safani mlembi, m'bwalo la kumtunda, pa khomo la chipata chatsopano cha nyumba ya Yehova, m'makutu a anthu onse. Pamene Mikaya mwana wa Gemariya, mwana wa Safani, anamva m'buku mau onse a Yehova, anatsikira kunyumba ya mfumu, nalowa m'chipinda cha mlembi; ndipo, taonani, akulu onse analikukhalamo, Elisama mlembi, ndi Delaya mwana wa Semaya, ndi Elinatani mwana wa Akibori, ndi Gemariya mwana wa Safani, ndi Zedekiya mwana wa Hananiya, ndi akulu onse. Ndipo Mikaya anafotokozera iwo mau onse amene anamva, pamene Baruki anawerenga buku m'makutu a anthu. Chifukwa chake akulu onse anatuma Yehudi mwana wa Netaniya, mwana wa Selemiya, mwana wa Kusi, kwa Baruki, kukanena, Tenga m'dzanja lako mpukutu wauwerenga m'makutu a anthu, nudze kuno. Ndipo Baruki mwana wa Neriya anatenga mpukutuwo m'dzanja lake, nadza kwa iwo. Ndipo anati kwa iye, Khala pansi tsopano, nuwerenga m'makutu athu. Ndipo Baruki anauwerenga m'makutu ao. Ndipo panali, pamene anamva mau onse, anaopa nayang'anana wina ndi mnzake, nati kwa Baruki, Tidzamfotokozeratu mfumu mau awa onse. Ndipo anamfunsa Baruki, kuti, Utifotokozeretu, Unalemba bwanji mau awa onse ponena iye? Ndipo Baruki anayankha iwo, Pakamwa pake ananditchulira ine mau awa onse, ndipo ndinawalemba ndi inki m'bukumo. Ndipo akulu anati kwa Baruki, Pita, nubisale iwe ndi Yeremiya; munthu yense asadziwe kumene muli. Ndipo analowa kwa mfumu kubwalo; ndipo anasunga buku m'chipinda cha Elisama mlembi; nafotokozera mau onse m'makutu a mfumu. Ndipo mfumu anatuma Yehudi atenge mpukutuwo; ndipo anautenga kutuluka nao m'chipinda cha Elisama mlembi. Ndipo Yehudi anauwerenga m'makutu a mfumu, ndi m'makutu a akulu onse amene anaima pambali pa mfumu. Ndipo mfumu anakhala m'nyumba ya nyengo yachisanu mwezi wachisanu ndi chinai; ndipo munali moto m'mbaula pamaso pake. Ndipo panali, pamene Yehudi anawerenga masamba atatu pena anai, mfumu inawadula ndi kampeni ka mlembi, niwaponya m'moto wa m'mbaulamo, mpaka mpukutu wonse unatha kupsa ndi moto wa m'mbaulamo. Ndipo sanaope, sanang'ambe nsalu zao, kapena mfumu, kapena atumiki ake aliyense amene anamva mau onsewa. Tsononso Elinatani ndi Delaya ndi Gemariya anapembedzera mfumu kuti asatenthe mpukutuwo; koma anakana kumvera. Ndipo mfumu inauza Yerameele mwana wake wa mfumu, ndi Seraya mwana wa Aziriele, ndi Selemiya mwana wa Abideele, kuti awagwire Baruki mlembi ndi Yeremiya mneneri; koma Yehova anawabisa. Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, mfumu itatentha mpukutuwo, ndi mau amene analemba Baruki ponena Yeremiya, kuti, Tenganso mpukutu wina, nulembe m'menemo mau oyamba aja anali mu mpukutu woyamba uja, umene Yehoyakimu mfumu ya Yuda wautentha. Ndipo za Yehoyakimu mfumu ya Yuda uziti, Yehova atero: Iwe watentha mpukutu uwu, ndi kuti, Bwanji walemba m'menemo, kuti, Mfumu ya ku Babiloni idzadzadi nidzaononga dziko ili, nidzatha m'menemo anthu ndi nyama? Chifukwa chake Yehova atero za Yehoyakimu mfumu ya Yuda: Adzasowa wokhala pa mpando wachifumu wa Davide; ndipo mtembo wake udzaponyedwa usana kunja kuli dzuwa, ndi usiku kuli chisanu. Ndipo ndidzamlanga iye ndi mbeu zake ndi atumiki ake chifukwa cha mphulupulu zao; ndipo ndidzawatengera iwo, ndi okhala m'Yerusalemu, ndi anthu a Yuda, zoipa zonse ndawanenera iwo, koma sanamvere. Ndipo Yeremiya anatenga mpukutu wina, naupereka kwa Baruki mlembi, mwana wa Neriya; amene analemba m'menemo ponena Yeremiya mau onse a m'buku lija Yehoyakimu mfumu ya Yuda analitentha m'moto; ndipo anaonjezapo mau ambiri oterewa. Ndipo Zedekiya mwana wa Yosiya anakhala mfumu m'malo a Koniya mwana wa Yehoyakimu, amene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni inamlowetsa mfumu m'dziko la Yuda. Koma ngakhale iye, ngakhale atumiki ake, ngakhale anthu a padziko, sanamvere mau a Yehova, amene ananena mwa Yeremiya mneneri. Ndipo Zedekiya mfumu anatuma Yehukala mwana wa Selemiya, ndi Zefaniya mwana wa Maaseiya wansembe, kwa Yeremiya mneneri, kukanena, Mutipemphereretu kwa Yehova Mulungu wathu. Ndipo Yeremiya analikuyendayenda mwa anthu; chifukwa asanamuike iye m'nyumba yandende. Ndipo nkhondo ya Farao inatuluka m'Ejipito; ndipo pamene Ababiloni omangira misasa Yerusalemu anamva mbiri yao, anachoka ku Yerusalemu. Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya mneneri, kuti, Atero Yehova, Mulungu wa Israele: Muzitero kwa mfumu ya Yuda, imene inakutumani inu kwa Ine kuti mundifunse Ine: Taonani, nkhondo ya Farao, yakutulukira kudzathandiza inu, idzabwerera ku Ejipito ku dziko lao. Ndipo Ababiloni adzabweranso, nadzamenyana ndi mudzi uwu; ndipo adzaulanda, nadzautentha ndi moto. Yehova atero: Musadzinyenge, kuti, Ababiloni adzatichokera ndithu; pakuti sadzachoka. Pakuti ngakhale mukadakantha nkhondo yonse ya Ababiloni akumenyana nanu, ngakhale akadatsala olasidwa okhaokha mwa iwo, koma iwowa akadauka yense m'hema wake ndi kutentha mudzi uwu ndi moto. Ndipo panali pamene nkhondo ya Ababiloni inachoka ku Yerusalemu chifukwa cha nkhondo ya Farao, pamenepo Yeremiya anatuluka m'Yerusalemu kumuka kudziko la Benjamini, kukalandira gawo lake kumeneko. Pokhala iye m'chipinda cha Benjamini, kapitao wa alonda anali kumeneko, dzina lake Iriya, mwana wa Selemiya, mwana wa Hananiya; ndipo iye anamgwira Yeremiya mneneri, nati, Ulinkupandukira kwa Ababiloni. Ndipo anati Yeremiya, Kunama kumeneko; ine sindipandukira kwa Ababiloni; koma sanamvere iye; ndipo Iriya anamgwira Yeremiya, nanka naye kwa akulu. Ndipo akulu anakwiyira Yeremiya, nampanda iye, namuika m'nyumba yandende m'nyumba ya Yonatani mlembi; pakuti anaiyesa ndende. Atafika Yeremiya kunyumba yadzenje, ku tizipinda take nakhalako Yeremiya masiku ambiri; pamenepo Zedekiya mfumu inatuma, ndi kumtenga iye; ndipo mfumu inamfunsa iye m'tseri m'nyumba mwake, niti, Kodi alipo mau ochokera kwa Yehova? Ndipo Yeremiya, anati, Alipo. Anatinso, Mudzaperekedwa m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni. Ndipo Yeremiya anati kwa mfumu Zedekiya, Ndachimwira inu chiyani, kapena atumiki anu, kapena anthu awa, kuti mwandiika m'nyumba yandende? Tsopano ali kuti aneneri anu, amene ananenera inu, kuti, Mfumu ya ku Babiloni sidzakudzerani inu, kapena dziko lino? Tsopano tamvanitu, mbuyanga mfumu; pembedzero langa ligwe pamaso panu; kuti musandibwezere kunyumba ya Yonatani mlembi, ndingafe kumeneko. Ndipo Zedekiya mfumu analamula, ndipo anamuika Yeremiya m'bwalo la kaidi, tsiku ndi tsiku, nampatsa mkate wofuma kumseu wa oumba mikate, mpaka unatha mkate wonse wa m'mudzi. Ndipo Yeremiya anakhala m'bwalo la kaidi. Ndipo Sefatiya mwana wa Matani ndi Gedaliya mwana wa Pusuri, ndi Yukala mwana wa Selemiya, ndi Pasuri mwana wa Malikiya, anamva mau amene Yeremiya ananena ndi anthu onse, kuti, Yehova atero, Iye wakukhala m'mudziwu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi chaola; koma iye wakutulukira kunka kwa Ababiloni adzakhala ndi moyo, ndipo adzakhala nao moyo wake ngati chofunkha, nadzakhala ndi moyo. Yehova atero, Mudziwu udzapatsidwatu m'dzanja la nkhondo ya mfumu ya ku Babiloni, ndipo adzaulanda. Ndipo akulu anati kwa mfumu, Munthu uyu aphedwetu; chifukwa analopetsa manja a anthu a nkhondo otsala m'mudzi uno, ndi manja a anthu onse, pakunena kwa iwo mau otero; pakuti munthu uyu safuna mtendere wa anthu awa, koma nsautso yao. Ndipo mfumu Zedekiya anati, Taonani, ali m'manja mwanu; pakuti mfumu singathe kuchita kanthu kotsutsana nanu. Ndipo anatenga Yeremiya, namponya iye m'dzenje la Malikiya mwana wake wa mfumu, limene linali m'bwalo la kaidi; ndipo anamtsitsa Yeremiya ndi zingwe. Koma m'dzenjemo munalibe madzi, koma thope; namira Yeremiya m'thopemo. Ndipo pamene Ebedemeleki Mkusi, mdindo, anamva kuti anamuika Yeremiya m'dzenje; mfumu ilikukhala pa chipata cha Benjamini; Ebedemeleki anatuluka m'nyumba ya mfumu, nanena ndi mfumu, kuti, Mbuyanga mfumu, anthu awa anachita zoipa m'zonse anachitira Yeremiya mneneri, amene anamponya m'dzenje; ndipo afuna kufa m'menemo chifukwa cha njala; pakuti mulibe chakudya china m'mudzimu. Ndipo mfumu inamuuza Ebedemeleki Mkusi, kuti, Tenga anthu makumi atatu, umkweze numtulutse Yeremiya mneneri m'dzenjemo, asanafe. Ndipo Ebedemeleki anatenga anthuwo, nalowa nao m'nyumba ya mfumu ya pansi pa nyumba ya chuma, natenga m'menemo nsalu zakale zotaya ndi zansanza zovunda, nazitsitsira ndi zingwe kwa Yeremiya m'dzenjemo. Ndipo Ebedemeleki Mkusi anati kwa Yeremiya, Kulungatu zingwe ndi nsaluzi zotaya zakale ndi zansanza ndi kuzikwapatira. Ndipo Yeremiya anachita chomwecho. Ndipo anamkweza Yeremiya ndi zingwe, namtulutsa m'dzenjemo; ndipo Yeremiya anakhalabe m'bwalo la kaidi. Ndipo mfumu Zedekiya anatuma, namtenga Yeremiya mneneri nalowa naye m'khomo lachitatu la nyumba ya Yehova; ndipo mfumu inati kwa Yeremiya, Ndidzakufunsa iwe kanthu; usandibisire ine kanthu. Ndipo Yeremiya anati kwa Zedekiya, Ndikakufotokozerani, kodi simudzandipha ine? Ndipo ndikakupangirani, simudzandimvera ine. Ndipo mfumu Zedekiya analumbira m'tseri kwa Yeremiya, kuti, Pali Yehova, amene anatilengera ife moyo uno, sindidzakupha iwe sindidzakupereka iwe m'manja mwa anthu awa amene afuna moyo wako. Ndipo Yeremiya anati kwa Zedekiya, Atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele: Ngati mudzatulukira kwa akulu a mfumu ya ku Babiloni, mudzakhala ndi moyo, ndipo mudziwu sudzatenthedwa ndi moto; ndipo mudzakhala ndi moyo ndi banja lanu; koma ngati simudzatulukira kwa akulu a mfumu ya ku Babiloni, mudziwu udzaperekedwa m'dzanja la Ababiloni, ndipo udzatenthedwa ndi moto, ndipo simudzapulumuka m'manja mwao. Ndipo mfumu Zedekiya anati kwa Yeremiya, Ine ndiopa Ayuda amene anandipandukira ine kunka kwa Ababiloni, angandipereke ine m'manja mwao, angandiseke. Koma Yeremiya anati, Sadzakuperekani. Mveranitu mau a Yehova, amene ndinena ndi inu, chomwecho kudzakomera inu, ndipo moyo wanu udzakhalabe. Koma ngati mukana kutuluka, mau anandisonyeza Yehova ndi awa: Taonani, akazi onse otsala m'nyumba ya mfumu ya Yuda adzatulutsidwa kunka kwa akulu a mfumu ya ku Babiloni, ndipo akaziwo adzati, Oyanjana nanu anakunyengani, ndi kukuposani inu, mapazi anu amire m'thope, abwerera m'mbuyo. Ndipo adzatulutsira Ababiloni akazi anu onse, ndi ana anu, ndipo simudzapulumuka m'manja ao, koma mudzagwidwa ndi dzanja la mfumu ya ku Babiloni; ndipo mudzatenthetsa mudziwu ndi moto. Ndipo Zedekiya anati kwa Yeremiya, Anthu asadziwe mau amene, ndipo sudzafa. Koma akamva akulu kuti ndalankhula ndi iwe, nakafika kwa iwe, ndi kuti kwa iwe, Utifotokozere ife chomwe wanena kwa mfumu; osatibisira ichi, ndipo sitidzakupha iwe; ndiponso zomwe mfumu inanena kwa iwe; pamenepo uziti kwa iwo, Ndinagwa ndi pembedzero langa pamaso pa mfumu, kuti asandibwezerenso kunyumba ya Yonatani ndifere komweko. Ndipo akulu onse anadza kwa Yeremiya, namfunsa; ndipo iye ananena nao monga mwa mau onsewo anamuuza mfumu. Ndipo analeka kunena naye; pakuti sikunamveka mlandu. Ndipo Yeremiya anakhala m'bwalo la kaidi mpaka tsiku lakugwidwa Yerusalemu. Ndipo anali komweko pogwidwa Yerusalemu. Chaka chachisanu ndi chinai cha Zedekiya mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi, anadza Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni ndi nkhondo yake yonse ku Yerusalemu, ndi kuumangira misasa. Chaka chakhumi ndi chimodzi cha Zedekiya, mwezi wachinai, tsiku lachisanu ndi chinai, mudzi unabooledwa. Ndipo akulu onse a mfumu ya ku Babiloni analowa, nakhala m'chipata chapakati, Neregali-Sarezere, Samugiri-Nebo, Sarisekimu, mkulu wa adindo, Nerigalisarezara mkulu wa alauli ndi akulu ena onse a mfumu ya ku Babiloni. Ndipo panali pamene Zedekiya mfumu ya Yuda ndi amuna onse a nkhondo anawaona, anathawa natuluka m'mudzi usiku, panjira pa munda wa mfumu, pa chipata cha pakati pa makoma awiri; ndipo iye anatulukira pa njira ya kuchidikha. Koma nkhondo ya Ababiloni inawalondola, nimpeza Zedekiya m'zidikha za Yeriko; ndipo atamgwira, anamtengera kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni ku Ribula m'dziko la Hamati, ndipo iye ananena naye mlandu. Pamenepo mfumu ya ku Babiloni inapha ana a Zedekiya ku Ribula pamaso pake; mfumu ya ku Babiloni niphanso aufulu onse a Yuda. Ndipo anakolowola maso a Zedekiya, nammanga m'zigologolo, kunka naye ku Babiloni. Ndipo Ababiloni anatentha ndi moto nyumba ya mfumu, ndi nyumba za anthu, nagumula malinga a Yerusalemu. Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga anthu otsalira m'mudzi, ndi othawa omwe, opandukira, ndi kumtsata ndi anthu otsalira nanka nao am'nsinga ku Babiloni. Koma aumphawi a anthu, amene analibe kanthu, Nebuzaradani kapitao wa alonda anawasiya m'dziko la Yuda, nawapatsa mipesa ndi minda nthawi yomweyo. Ndipo Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anamuuza Nebuzaradani kapitao wa alonda, za Yeremiya, kuti, Umtenge, numyang'anire bwino, usamsautse, koma umchitira monga iye adzanena nawe. Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatumiza, ndi Nebusazibani, mkulu wa adindo Rabi-Sarisi, ndi Neregali-Sarezere mkulu wa alauli, ndi akulu onse a mfumu ya ku Babiloni; iwonso anatumiza, namchotsa Yeremiya m'bwalo la kaidi, nampereka iye kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, kuti anke naye kwao; momwemo iye anakhala ndi anthu. Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, potsekeredwa iye m'bwalo la kaidi, kuti, Pita, ukanene kwa Ebedemeleki Mkusi, kuti, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Taona, ndidzafikitsira mudzi uwu mau anga kuusautsa, osauchitira zabwino; ndipo adzachitidwa pamaso pako tsiku lomwelo. Koma ndidzakupulumutsa tsiku lomwelo, ati Yehova: ndipo sudzaperekedwa m'manja a anthu amene uwaopa. Pakuti ndidzakupulumutsatu ndipo sudzagwa ndi lupanga, koma udzakhala nao moyo wako ngati chofunkha, pakuti wandikhulupirira Ine, ati Yehova. Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, Nebuzaradani kapitao wa alonda atammasula pa Rama, pamene anamtenga iye womangidwa m'maunyolo pamodzi ndi am'nsinga onse a Yerusalemu ndi Yuda, amene anatengedwa am'nsinga kunka nao ku Babiloni. Ndipo kapitao wa alonda anatenga Yeremiya, nati kwa iye, Yehova Mulungu wako ananenera choipa ichi malo ano; ndipo Yehova wachitengera, ndi kuchita monga ananena, chifukwa mwachimwira Yehova, ndi kusamvera mau ake, chifukwa chake chinthu ichi chakufikirani. Ndipo tsopano, taona, ndikumasula iwe lero maunyolo ali pa manja ako. Kukakukomera kudza nane ku Babiloni, idza, ndipo ndidzakusamalira bwino; koma kukakuipira kudza nane ku Babiloni, tsala; taona, dziko lonse lili pamaso pako; kulikonse ukuyesa kwabwino kapena koyenera kupitako, pita kumeneko. Tsono asanabwerere iye anati, Bweratu kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, amene mfumu ya ku Babiloni inamyesa wolamulira midzi ya Yuda, nukhale naye pakati pa anthu; kapena pita kulikonse ukuyesa koyenera kupitako. Ndipo kapitao wa alonda anampatsa iye phoso ndi mtulo, namleka amuke. Ndipo Yeremiya ananka kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa, nakhala kumeneko kwa anthu otsala m'dziko. Ndipo pamene akulu onse a makamu amene anali m'minda, iwo ndi anthu ao, anamva kuti mfumu ya ku Babiloni adamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu wolamulira dziko, nampatsira amuna, ndi akazi, ndi ana, ndi aumphawi a m'dzikomo, a iwo amene sanatengedwe ndende kunka nao ku Babiloni; pamenepo anadza kwa Gedaliya ku Mizipa, Ismaele mwana wa Netaniya, ndi Yohanani ndi Yonatani ana a Kareya, ndi Seraya mwana wa Tanumeti, ndi ana a Efayi wa ku Netofa, ndi Yezaniya mwana wa munthu wa ku Maaka, iwo ndi anthu ao. Ndipo Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani anawalumbirira iwo ndi anthu ao, kuti, Musaope kuwatumikira Ababiloni; khalani m'dzikomu, mutumikire mfumu ya ku Babiloni, ndipo kudzakukomerani. Koma ine, taonani, ndidzakhala pa Mizipa, ndiima pamaso pa Ababiloni, amene adzadza kwa ife; koma inu sonkhanitsani vinyo ndi zipatso zamalimwe ndi mafuta, muziike m'mbiya zanu, nimukhale m'midzi imene mwailanda. Chomwecho pamene Ayuda onse okhala m'Mowabu ndi mwa ana a Amoni, ndi m'Edomu, ndi amene anali m'maiko monse, anamva kuti mfumu ya ku Babiloni inasiya otsala a Yuda, ndi kuti inamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani wolamulira wao; pamenepo Ayuda onse anabwerera kufumira ku malo onse kumene anawaingitsirako, nafika ku dziko la Yuda, kwa Gedaliya, ku Mizipa, nasonkhanitsa vinyo ndi zipatso zamalimwe zambiri. Ndiponso Yohanani mwana wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo okhala m'minda, anadza kwa Gedaliya ku Mizipa, nati kwa iye, Kodi mudziwa kuti Baalisi mfumu ya ana a Amoni watumiza Ismaele mwana wa Netaniya kuti akupheni inu? Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu sanamvere iwo. Ndipo Yohanani mwana wa Kareya ananena kwa Gedaliya ku Mizipa m'tseri, kuti, Ndimuketu, ndikaphe Ismaele mwana wa Netaniya, anthu osadziwa; chifukwa chanji adzakuphani inu, kuti Ayuda onse amene anakusonkhanira inu amwazike, ndi otsala a Yuda aonongeke? Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu anati kwa Yohanani mwana wa Kareya, Usachite ichi; pakuti unamizira Ismaele. Ndipo panali mwezi wachisanu ndi chiwiri, Ismaele mwana wa Netaniya, mwana wa Elisama, wa mbeu ya mfumu, ndi kapitao wamkulu wa mfumu, ndi anthu khumi pamodzi ndi iye, anadza kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa; pamenepo anadya pamodzi m'Mizipa. Ndipo anauka Ismaele mwana wa Netaniya, ndi anthu khumi okhala naye, namkantha Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani ndi lupanga, namupha iye, amene mfumu ya ku Babiloni inamuika wolamulira dziko. Ismaele naphanso Ayuda onse okhala naye Gedaliya pa Mizipa, ndi Ababiloni amene anakomana nao komweko, amuna a nkhondo. Ndipo panali atapita masiku awiri atamupha Gedaliya, anthu osadziwa, anadza anthu ochokera ku Sekemu, ndi ku Silo, ndi ku Samariya, anthu makamu asanu ndi atatu, atameta ndevu zao, atang'amba zovala zao, atadzitematema, anatenga nsembe zaufa ndi lubani m'manja mwao, kunka nazo kunyumba ya Yehova. Ndipo Ismaele mwana wa Netaniya anatuluka m'Mizipa kukakomana nao, alinkuyenda ndi kulira misozi; ndipo panali, pamene anakomana nao, anati kwa iwo, Idzani kwa Gedaliya mwana wake wa Ahikamu. Ndipo panali, pamene analowa pakati pa mudzi, Ismaele mwana wa Netaniya anawapha, nawaponya pakati pa dzenje, iye ndi anthu okhala naye. Koma mwa iwo anaoneka anthu khumi amene anati kwa Ismaele, Musatiphe ife; pakuti tili ndi chuma chobisika m'mudzi, cha tirigu, ndi cha barele, ndi cha mafuta, ndi cha uchi. Momwemo analeka, osawapha pakati pa abale ao. Ndipo dzenje moponyamo Ismaele mitembo yonse ya anthu amene anawapha, chifukwa cha Gedaliya, ndilo analipanga mfumu Asa chifukwa cha kuopa Baasa mfumu ya Israele, lomwelo Ismaele mwana wa Netaniya analidzaza ndi ophedwawo. Ndipo Ismaele anatenga ndende otsala onse a anthu okhala m'Mizipa, ana akazi a mfumu, ndi anthu onse amene anatsala m'Mizipa, amene Nebuzaradani kapitao wa alonda anapatsira Gedaliya mwana wa Ahikamu; Ismaele mwana wa Netaniya anawatenga ndende, napita kukaolokera kwa ana a Amoni. Koma pamene Yohanani mwana wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo akhala naye, anamva zoipa zonse anazichita Ismaele mwana wa Netaniya, anatenga anthu onse, nanka kukamenyena ndi Ismaele mwana wa Netaniya, nampeza pa madzi ambiri a m'Gibiyoni. Ndipo panali pamene anthu onse amene anali ndi Ismaele anaona Yohanani mwana wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo okhala naye, anasekera. Ndipo anthu onse amene Ismaele anatenga ndende kuwachotsa m'Mizipa anatembenuka nabwera, nanka kwa Yohanani mwana wake wa Kareya. Koma Ismaele mwana wake wa Netaniya anapulumuka Yohanani ndi anthu asanu ndi atatu, nanka kwa ana a Amoni. Ndipo Yohanani mwana wake wa Kareya ndi akazembe onse a makamu amene anali naye, anatenga anthu onse otsala a ku Mizipa, amene anawabweza kwa Ismaele mwana wake wa Netaniya atapha Gedaliya mwana wake wa Ahikamu, anthu a nkhondo, ndi akazi, ndi ana, ndi adindo, amene anawabwezanso ku Gibiyoni; ndipo anachoka, natsotsa m'Geruti-Kimuhamu, amene ali ku Betelehemu, kunka kulowa m'Ejipito, chifukwa cha Ababiloni; pakuti anawaopa, chifukwa Ismaele mwana wake wa Netaniya anapha Gedaliya mwana wake wa Ahikamu, amene mfumu ya ku Babiloni anamuika wolamulira m'dzikomo. Ndipo akazembe onse a nkhondo, ndi Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi Yezaniya mwana wake wa Hosaya, ndi anthu onse kuyambira wamng'ono, kufikira wamkulu, anayandikira, nati kwa Yeremiya mneneri, Chipembedzero chathu chigwe pamaso panu, nimutipempherere ife kwa Ambuye Mulungu wanu, chifukwa cha otsala onsewa; pakuti tatsala ife owerengeka m'malo mwa ambiri, monga maso anu ationa ife; kuti Yehova Mulungu wanu atisonyeze ife njira imene tiyendemo, ndi chomwe tichite. Ndipo Yeremiya mneneri anati kwa iwo, Ndamva; taonani, ndidzapemphera kwa Yehova Mulungu wanu monga mwa mau anu; ndipo padzakhala kuti chilichonse Yehova adzakuyankhirani, ndidzakufotokozerani; sindidzakubisirani inu kanthu. Pamenepo iwo anati kwa Yeremiya, Yehova akhale mboni yoona ndi yokhulupirika pakati pa ife, ngati sitichita monga mwa mau onse Yehova Mulungu wanu adzakutumizani nao kwa ife. Ngakhale ali abwino, ngakhale ali oipa, ife tidzamvera mau a Yehova Mulungu wathu, kwa Iye amene tikutumizani inu; kuti kutikomere, pomvera mau a Yehova Mulungu wathu. Ndipo panali atapita masiku khumi, mau a Yehova anadza kwa Yeremiya. Ndipo anaitana Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo okhala naye, ndi anthu onse kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu, nati kwa iwo, Atero Yehova, Mulungu wa Israele, kwa Iye amene munandituma ine ndigwetse pembedzero lanu pamaso pake, Ngati mudzakhalabe m'dziko muno, ndidzamangitsa mudzi wanu, osakugumulani, ndidzakuokani inu, osakuzulani; pakuti ndagwidwa nacho chisoni choipa chimene ndakuchitirani inu. Musaope mfumu ya ku Babiloni, amene mumuopa; musamuope, ati Yehova: pakuti Ine ndili ndi inu kukupulumutsani, ndi kukulanditsani m'dzanja lake. Ndipo ndidzakuchitirani inu chifundo, kuti iye akuchitireni inu chifundo, nakubwezereni inu kudziko lanu. Koma mukati, Sitidzakhala m'dziko muno; osamvera mau a Yehova Mulungu wanu; ndi kuti, Iai; tidzanka ku Ejipito, kumene sitidzaona nkhondo, sitidzamva kulira kwa lipenga, sitidzamva njala yokhumba mkate; pamenepo tidzakhala; chifukwa chake mumve mau a Yehova, Otsala inu a Yuda, atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Ngati mulozetsa nkhope zanu kuti mulowe m'Ejipito, kukakhala m'menemo; pamenepo padzakhala, kuti lupanga limene muopa lidzakupezani m'menemo m'dziko la Ejipito, ndi njala, imene muiopa, idzakuumirirani kumeneko ku Ejipito; pamenepo mudzafa. Kudzatero ndi anthu onse akulozetsa nkhope zao anke ku Ejipito kuti akhale kumeneko; adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi chaola; ndipo wa iwo sadzatsala kapena kupulumuka ku choipa chimene ndidzatengera pa iwo ngakhale mmodzi yense. Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Monga mkwiyo wanga ndi ukali wanga wathiridwa kwa okhala m'Yerusalemu, momwemo ukali wanga udzathiridwa pa inu, pamene mudzalowa m'Ejipito; ndipo mudzakhala chitukwano, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, ndi chitonzo; ndipo simudzaonananso malo ano. Yehova wanena za inu, otsala inu a Yuda, Musalowe m'Ejipito; mudziwetu kuti ndakulangizani inu lero. Pakuti mwanyenga m'miyoyo yanu; pakuti mwandituma ine kwa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Mutipempherere ife kwa Yehova Mulungu wathu; ndipo monga mwa zonse Yehova Mulungu wathu adzanena, momwemo mutifotokozere ife; ndipo tidzachita. Ndipo lero ndakufotokozerani, ndipo simunamva mau a Yehova Mulungu wanu m'chinthu chilichonse chimene Iye wanditumira ine nacho kwa inu. Tsopano mudziwetu kuti mudzafa ndi lupanga, ndi njala ndi chaola, komwe mufuna kukakhalako. Ndipo panali pamene Yeremiya anatha kunena kwa anthu onse mau onse a Yehova Mulungu wao, amene anamtuma iye nao Yehova Mulungu wao, mau onse amenewo, pamenepo ananena Azariya mwana wake wa Hosaya, ndi Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi anthu onse odzikuza, nati kwa Yeremiya, Unena zonama; Yehova Mulungu wathu sanakutumize iwe kudzanena, Musalowe m'Ejipito kukhala m'menemo; koma Baruki mwana wake wa Neriya atichichizira inu, mutipereke m'dzanja la Ababiloni, kuti atiphe ife, atitengere ife am'nsinga ku Babiloni. Ndipo Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo, ndi anthu onse sanamvere mau a Yehova, kuti akhale m'dziko la Yuda. Koma Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo, anatenga otsala onse a Yuda, amene anabwera kumitundu yonse kumene anaingitsidwirako kuti akhale m'dziko la Yuda; ndi amuna, ndi akazi, ndi ana, ndi ana akazi a mfumu, ndi anthu onse amene Nebuzaradani kapitao wa alonda anasiya ndi Gedaliya mwana wake wa Ahikamu, mwana wake wa Safani, ndi Yeremiya mneneri, ndi Baruki mwana wake wa Neriya; ndipo anadza nalowa m'dziko la Ejipito; pakuti sanamvere mau a Yehova; ndipo anadza mpaka ku Tapanesi. Ndipo anafika mau a Yehova kwa Yeremiya m'Tapanesi, kuti, Tenga miyala yaikulu m'dzanja lako, nuiyale ndi dothi pakati pa njerwa, za pa khomo la nyumba ya Farao m'Tapanesi pamaso pa anthu a Yuda; ndi kuti kwa iwo, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Taonani Ine ndidzatuma ndidzatenga Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndi kuika mpando wake wachifumu pa miyalayi ndaiyala; ndipo iye adzaivundikira ndi hema wachifumu wake. Ndipo iye adzafika, nadzakantha dziko la Ejipito; nadzapereka kuimfa iwo a kuimfa, ndi kundende iwo a kundende, ndi kulupanga iwo a kulupanga. Ndidzayatsa moto m'nyumba za milungu ya Ejipito; ndipo adzazitentha, nadzaitenga ndende; ndipo adzadzifunda ndi dziko la Ejipito, monga mbusa avala chovala chake; nadzatuluka m'menemo ndi mtendere. Ndipo adzathyola mizati ya zoimiritsa za Kachisi wa dzuwa, ali m'dziko la Ejipito; ndi nyumba za milungu ya Aejipito adzazitentha ndi moto. Mau amene anadza kwa Yeremiya onena za Ayuda onse amene anakhala m'dziko la Ejipito, okhala pa Migidoli, ndi pa Tapanesi, ndi pa Nofi, ndi m'dziko la Patirosi, akuti, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Mwaona choipa chonse chimene ndatengera pa Yerusalemu, ndi pa midzi yonse ya Yuda; ndipo, taonani, lero lomwe ili bwinja, palibe munthu wokhalamo; chifukwa cha choipa chao anachichita kuutsa nacho mkwiyo wanga; pakuti anapita kukafukizira, ndi kutumikira milungu ina, imene sanaidziwe, ngakhale iwo, ngakhale inu, ngakhale makolo anu. Koma ndinatuma kwa inu atumiki anga onse aneneri, ndinauka mamawa ndi kuwatuma, ndi kuti, Musachitetu chonyansa ichi ndidana nacho. Koma sanamvere, sanatchere khutu lao kuti atembenuke asiye choipa chao, osafukizira milungu ina. Chifukwa chake mkwiyo wanga ndi ukali wanga unathiridwa, nuyaka m'midzi ya Yuda ndi m'miseu ya Yerusalemu; ndipo yapasudwa nikhala bwinja, monga lero lomwe. Ndipo tsopano atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele: Chifukwa chanji muchitira miyoyo yanu choipa ichi, kudzisadzira nokha amuna ndi akazi, makanda ndi oyamwa, pakati pa Yuda, osakusiyirani mmodzi yense; popeza muutsa mkwiyo wanga ndi ntchito ya manja anu, pofukizira milungu ina m'dziko la Ejipito, kumene mwapita kukhalako; kuti mudulidwe, ndi kuti mukhale chitemberero ndi chitonzo mwa amitundu onse a dziko lapansi? Kodi mwaiwala zoipa za makolo anu, ndi zoipa za mafumu a Yuda, ndi zoipa za akazi ao, ndi zoipa zanu, ndi za akazi anu, zimene anazichita m'dziko la Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu? Sanadzichepetse mpaka lero lomwe, sanaope, sanayende m'chilamulo changa, kapena m'malemba anga, amene ndinaika pamaso panu ndi pa makolo anu. Chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Taonani, ndidzayang'anitsa nkhope yanga pa inu ndikuchitireni inu choipa, ndidule Yuda lonse. Ndipo ndidzatenga otsala a Yuda, amene analozetsa nkhope zao alowe m'dziko la Ejipito akhale m'menemo, ndipo adzathedwa onse; m'dziko la Ejipito adzagwa, adzathedwa ndi lupanga ndi njala; adzafa kuyambira wamng'ono mpaka wamkulu, ndi lupanga ndi njala; ndipo adzakhala chitukwano, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, ndi chitonzo. Ndipo ndidzalanga iwo okhala m'dziko la Ejipito, monga ndinalanga Yerusalemu, ndi lupanga, ndi njala, ndi chaola; kuti otsala a Yuda, amene ananka kudziko la Ejipito kukhala m'menemo, asapulumuke asatsale ndi mmodzi yense, kuti abwere kudziko la Yuda, kumene afuna kubwera kuti akhale m'menemo; pakuti adzabwera koma adzapulumuka ndiwo. Ndipo amuna onse amene anadziwa kuti akazi ao anafukizira milungu ina, ndi akazi onse omwe anaimirirapo, msonkhano waukulu, anthu onse okhala m'dziko la Ejipito, m'Patirosi, anamyankha Yeremiya, kuti, Koma mau amene wanena ndi ife m'dzina la Yehova, sitidzakumvera iwe. Koma tidzachita ndithu mau onse anatuluka m'kamwa mwathu, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, monga momwe tikachitira ife, ndi atate athu, ndi mafumu athu ndi akulu athu, m'midzi ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, pakuti pamenepo tinali ndi chakudya chokwanira, tinakhala bwino, sitinaona choipa. Koma chilekere ife kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira, tasowa zonse, tathedwa ndi lupanga ndi chaola. Ndipo pamene tinafukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira nsembe zothira, kodi tinamuumbira iye mikate yakumpembedzera, ndi kumthirira nsembe zothira, opanda amuna athu? Ndipo Yeremiya anati kwa anthu onse, kwa amuna, ndi kwa akazi, kwa anthu onse amene anambwezera mau amenewa, ndi kuti, Zofukizira zanu m'midzi ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, za inu ndi atate anu, mafumu anu ndi akulu anu, ndi anthu a m'dziko, kodi Yehova sanazikumbukire, kodi sizinalowe m'mtima mwake? Ndipo Yehova sanathe kupirirabe, chifukwa cha machitidwe anu oipa, ndi chifukwa cha zonyansa zimene munazichita; chifukwa chake dziko lanu likhala bwinja, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, lopanda wokhalamo, monga lero lomwe. Chifukwa mwafukiza, ndi chifukwa mwachimwira Yehova, osamvera mau a Yehova, osayenda m'chilamulo chake, ndi m'malemba ake, ndi m'mboni zake, chifukwa chake choipachi chakugwerani, monga lero lomwe. Ndiponso Yeremiya anati kwa anthu onse, ndi kwa akazi onse, Tamvani mau a Yehova, nonse Ayuda amene muli m'dziko la Ejipito. Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Inu ndi akazi anu mwanena ndi m'kamwa mwanu, ndi kukwaniritsa ndi manja anu kuti, Tidzachita ndithu zowinda zathu taziwindira, kufukizira mfumu yaikazi ya kumwamba, ndi kumthirira iye nsembe zothira; khazikitsanitu zowinda zanu, chitani zowinda zanu. Chifukwa chake tamvani mau a Yehova, nonse Ayuda okhala m'dziko la Ejipito: Taonani, ndalumbira, Pali dzina langa lalikulu, ati Yehova, kuti dzina langa silidzatchulidwanso m'kamwa mwa munthu aliyense wa Yuda m'dziko la Ejipito, ndi kuti, Pali Yehova Mulungu. Taonani, ndiwayang'anira kuwachitira zoipa, si zabwino; ndipo amuna onse a Yuda okhala m'dziko la Ejipito adzathedwa ndi lupanga ndi njala, mpaka kutha kwao. Ndipo iwo amene adzapulumuka kulupanga adzabwera kutuluka kudziko la Ejipito kulowa m'dziko la Yuda, owerengeka; ndipo otsala onse a Yuda, amene analowa m'dziko la Ejipito kuti akhale m'menemo, adzadziwa ngati adzatsimikizidwa mau a yani, kapena anga, kapena ao. Ndipo ichi chidzakhala chizindikiro cha kwa inu, ati Yehova, chakuti Ine ndidzakulangani m'malo muno, kuti mudziwe kuti mau anga adzatsimikizidwatu akuchitireni inu zoipa. Yehova atero: Taonani, ndidzapereka Farao Hofira mfumu ya Aejipito m'manja a adani ake, ndi m'manja a iwo akufuna moyo wake; monga ndinapereka Zedekiya mfumu ya Yuda m'manja a Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni mdani wake, amene anafuna moyo wake. Mau amene ananena Yeremiya mneneri kwa Baruki mwana wake wa Neriya, pamene analemba mau awa m'buku ponena Yeremiya, chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, ndi kuti, Yehova Mulungu wa Israele atero kwa inu, Baruki: Munati, Kalanga ine tsopano! Pakuti Yehova waonjezera chisoni pa zowawa zanga; ndalema ndi kubuula kwanga, sindipeza kupuma. Uzitero naye, Yehova atero: Taonani, chimene ndamanga ndidzapasula, ndi chimene ndaoka ndidzazula; ndidzatero m'dziko lonseli. Kodi udzifunira wekha zinthu zazikulu? Usazifune; pakuti, taona, ndidzatengera zoipa pa anthu onse, ati Yehova: koma moyo wako ndidzakupatsa iwe ngati chofunkha m'malo monse m'mene mupitamo. Mau a Yehova amene anadza kwa Yeremiya mneneri akunena za amitundu. Za Ejipito: kunena za nkhondo ya Farao Neko mfumu ya Aejipito, imene inali pa mtsinje wa Yufurate m'Karikemisi, imene anaikantha Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni chaka chachinai cha Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda. Konzani chikopa ndi lihawo, nimuyandikire kunkhondo. Mangani akavalo, bwerani, inu apakavalo, imani ndi zisoti zazitsulo; tuulani nthungo zanu, valani malaya achitsulo. Chifukwa chanji ndachiona? Aopa, abwerera; amphamvu ao agwetsedwa, athawadi, osacheukira m'mbuyo; mantha ali ponseponse, ati Yehova. Waliwiro asathawe, wamphamvu asapulumuke; kumpoto pambali pa mtsinje wa Yufurate waphunthwa nagwa. Ndani uyu amene auka ngati Nailo, madzi ake ogavira monga nyanja? Ejipito auka ngati Nailo, madzi ake agavira ngati nyanja; ndipo ati, Ndidzauka, ndidzamiza dziko lapansi; ndidzaononga mudzi ndi okhalamo ake. Kwerani, inu akavalo; chitani misala, inu magaleta, atuluke amphamvu; Akusi ndi Aputi, ogwira chikopa; ndi Aludi, amene agwira ndi kukoka uta. Pakuti tsikulo ndi la Ambuye, Yehova wa makamu, tsiku lakubweza chilango, kuti abwezere chilango adani ake; ndipo lupanga lidzadya, lidzakhuta, nilidzamwetsa mwazi wao; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, ali ndi nsembe m'dziko la kumpoto pa mtsinje wa Yufurate. Kwera ku Giliyadi, tenga vunguti, namwali iwe mwana wa Ejipito; wachulukitsa mankhwala chabe; palibe kuchira kwako. Amitundu amva manyazi anu, dziko lapansi ladzala ndi kufuula kwanu; pakuti amphamvu akhumudwitsana, agwa onse awiri pamodzi. Mau amene Yehova ananena kwa Yeremiya mneneri, kuti Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adzafika adzakantha dziko la Ejipito. Nenani m'Ejipito, lalikirani m'Migidoli, lalikirani m'Nofi ndi Tapanesi; nimuti, Udziimike, nudzikonzere wekha; pakuti lupanga ladya pozungulira pako. Akulimba ako akokoledwa bwanji? Sanaime, chifukwa Yehova anawathamangitsa. Anaphunthwitsa ambiri, inde, anagwa wina pa mnzake, ndipo anati, Ukani, tinkenso kwa anthu athu, kudziko la kubadwa kwathu, kuchokera kulupanga lovutitsa. Ndipo anafuula kumeneko, Farao mfumu ya Aejipito ndiye phokoso lokha; wapititsa nthawi yopangira. Pali Ine, ati Mfumu, dzina lake ndi Yehova wa makamu, ndithu monga Tabori mwa mapiri, monga Karimele pambali pa nyanja, momwemo adzafika. Mwana wamkazi iwe wokhala m'Ejipito, dzikonzere kunka kundende; pakuti Nofi adzakhala bwinja, nadzapsa, mulibenso wokhalamo. Ejipito ndi ng'ombe yaikazi yosalala; chionongeko chituluka kumpoto chafika, chafika. Ndiponso olipidwa ake ali pakati pake onga ngati anaang'ombe a m'khola; pakuti iwonso abwerera, athawa pamodzi, sanaime; pakuti tsiku la tsoka lao linawafikira, ndi nthawi ya kuweruzidwa kwao. Mkokomo wake udzanga wa njoka yothawa; pakuti adzayenda ndi nkhondo, adzafika kumenyana naye ndi nkhwangwa, monga akutema mitengo. Adzatema nkhalango yake, ati Yehova, pokhala yosapitika; pakuti achuluka koposa dzombe, ali osawerengeka. Mwana wake wamkazi wa Ejipito adzachitidwa manyazi, adzaperekedwa m'manja a anthu a kumpoto. Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, ati: Taonani, ndidzalanga Amoni wa No, ndi Farao, ndi Ejipito, pamodzi ndi milungu yake, ndi mafumu ake; ngakhale Farao, ndi iwo akumkhulupirira iye; ndipo ndidzawapereka m'manja a iwo amene afuna moyo wao, ndi m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndi m'manja a atumiki ake; pambuyo pake adzakhalamo anthu, monga masiku akale, ati Yehova. Koma usaope iwe, mtumiki wanga Yakobo, usachite mantha, iwe Israele: pakuti, taona, ndidzakupulumutsa iwe kuchokera kutali, ndi mbeu yako kudziko la undende wao, ndipo Yakobo adzabwera, nadzapumula m'mtendere, ndipo palibe amene adzamuopetsa iye. Usaope, iwe Yakobo mtumiki wanga, ati Yehova; pakuti Ine ndili ndi iwe; pakuti Ine ndidzathetsa mitundu yonse kumene ndinakuingitsirako iwe, koma sindidzakuthetsa iwe; koma ndidzakulangiza ndi chiweruziro, ndipo sindidzakusiya konse wosalangidwa. Mau a Yehova amene anadza kwa Yeremiya mneneri onena za Afilisti, Farao asanakanthe Gaza. Yehova atero: Taonani, madzi adzakwera kutuluka kumpoto, nadzakhala mtsinje wosefuka, nadzasefukira padziko ndi pa zonse zili m'mwemo, pamudzi ndi pa onse okhalamo; ndipo amuna adzalira, ndi onse okhala m'dziko adzakuwa. Pomveka migugu ya ziboda za olimba ake, pogumukira magaleta ake, ndi pophokosera njinga zake, atate sadzacheukira ana ao chifukwa cha kulefuka kwa manja ao; chifukwa cha tsiku lakudzafunkha Afilisti onse, kuphera Tiro ndi Sidoni othangata onse akutsala; pakuti Yehova adzafunkha Afilisti, otsala a chisumbu cha Kafitori. Dazi lafikira a Gaza; Asikeloni wathedwa, otsala m'chidikha chao; udzadzicheka masiku angati? Iwe lupanga la Yehova, atsala masiku angati osakhala chete iwe? Dzilonge wekha m'chimake; puma, nukhale chete. Udzakhala chete bwanji, popeza Yehova anakulangiza? Za Asikeloni, ndi za m'mphepete mwa nyanja, pamenepo analiika. Za Mowabu. Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Tsoka Nebo! Pakuti wapasuka; Kiriyataimu wachitidwa manyazi, wagwidwa; linga la pamtunda lachitidwa manyazi lapasudwa. Palibenso kutamanda Mowabu; m'Hesiboni anamlingiririra zoipa, ndi kuti, Tiyeni, tiwathe asakhalenso mtundu wa anthu. Iwenso, Madimeni, udzatontholetsedwa, lupanga lidzakulondola iwe. Mau amveka kuchokera ku Horonaimu, kufunkha ndi kuononga kwakukulu! Mowabu waonongedwa; ang'ono ake amveketsa kulira. Pakuti adzakwera pa chikweza cha Luhiti ndi kulira kosaleka; pakuti pa chitsiko cha Horonaimu amva kulira kowawa kwa chionongeko. Thawani, pulumutsani miyoyo yanu, mukhale amaliseche m'chipululu. Pakuti, chifukwa wakhulupirira ntchito zanu ndi chuma chanu, iwenso udzagwidwa; ndipo Kemosi adza kundende, ansembe ake ndi akulu ake pamodzi. Ndipo wakufunkha adzafikira pa midzi yonse, sudzapulumuka mudzi uliwonse; chigwa chomwe chidzasakazidwa, ndipo chidikha chidzaonongedwa; monga wanena Yehova. Patsani Mowabu mapiko, kuti athawe apulumuke; midzi yake ikhale bwinja, lopanda wokhalamo. Atembereredwe iye amene agwira ntchito ya Yehova monyenga, atembereredwe iye amene abweza lupanga lake kumwazi. Mowabu wakhala m'mtendere kuyambira ubwana wake, wakhala pansenga, osatetekulidwa, sananke kundende; chifukwa chake makoleredwe ake alimobe mwa iye, fungo lake silinasinthika. Chifukwa chake, taonani, masiku adza, ati Yehova, amene ndidzatuma kwa iye otsanula, amene adzamtsanula iye; adzataya za mbiya zake, nadzaswa zipanda zao. Ndipo Mowabu adzachita manyazi chifukwa cha Kemosi, monga nyumba ya Israele inachita manyazi chifukwa cha Betele amene anamkhulupirira. Muti bwanji, Tili amphamvu, olimba mtima ankhondo? Mowabu wapasuka, akwera kulowa m'midzi yake, ndi anyamata ake osankhika atsikira kukaphedwa, ati Mfumu, dzina lake ndiye Yehova wa makamu. Tsoka la Mowabu layandikira kudza, nsautso yake ifulumiratu. Inu nonse akumzungulira, mumchitire iye chisoni, inu nonse akudziwa dzina lake; muti, Chibonga cholimba chathyokatu, ndodo yokoma! Iwe mwana wamkazi wokhala m'Diboni, utsike pa ulemerero wako, nukhale ndi ludzu; pakuti wakufunkha Mowabu wakukwerera, iwe waononga malinga ako. Iwe wokhala m'Aroere, ima panjira, nusuzumire umfunse iye amene athawa, ndi mkazi amene apulumuka; nuti, Chachitidwa chiyani? Mowabu wachitidwa manyazi, pakuti wathyoka; kuwa nulire, nunene m'Arinoni, kuti Mowabu wapasuka. Chiweruzo chafika pa dziko lachidikha; pa Holoni, ndi pa Yahazi, ndi pa Mefaati; ndi pa Diboni, ndi pa Nebo, ndi pa Betedibilataimu; ndi pa Kiriyataimu, ndi pa Betegamuli, ndi pa Betemeoni; ndi pa Keriyoti, ndi pa Bozira, ndi pa midzi yonse ya dziko la Mowabu, yakutali kapena yakufupi. Nyanga ya Mowabu yaduka, ndipo wathyoka mkono wake, ati Yehova. Umledzeretse iye; pakuti anadzikuza pokana Yehova; Mowabu yemwe adzavimvinika m'kusanza kwake, ndipo iye adzasekedwanso. Kodi sunaseka Israele? Kodi iye anapezedwa mwa mbala? Pakuti nthawi zonse unena za iye, upukusa mutu. Inu okhala m'Mowabu, siyani midzi, khalani m'thanthwe; nimukhale monga njiwa imene isanja chisanja chake pambali pakamwa pa dzenje. Ife tamva kudzikuza kwa Mowabu, wadzikuza ndithu, kunyang'wa kwake, ndi kunyada kwake, ndi kudzitama kwake, ndi kudzikuza kwa mtima wake. Ine ndidziwa mkwiyo wake, ati Yehova, kuti uli chabe; zonyenga zake sizinachita kanthu. Chifukwa chake ndidzakuwira Mowabu; inde, ndidzafuulira Mowabu yense, adzalirira anthu a ku Kiriheresi. Iwe mpesa wa Sibima; ndidzakulirira iwe ndi kulira kopambana kulira kwa Yazere, nthambi zako zinapitirira nyanja, zinafikira kunyanja ya Yazere; wakufunkha wagwera zipatso zako za mpakasa ndi mphesa zako. Ndipo kusekera ndi kukondwa kwachotsedwa, kumunda wobala ndi kudziko la Mowabu; ndipo ndaletsa vinyo pa zoponderamo; sadzaponda ndi kufuula; kufuula sikudzakhala kufuula. Kuyambira kufuula kwa Hesiboni mpaka ku Eleyale, mpaka ku Yahazi anakweza mau, kuyambira pa Zowari mpaka ku Horonaimu, ku Egilati-Selisiya; pakuti pa madzi a ku Nimurimu komwe padzakhala mabwinja. Ndiponso ndidzaletsa m'Mowabu, ati Yehova, iye amene apereka nsembe pamsanje, ndi iye amene afukizira milungu yake. Chifukwa chake mtima wanga umlirira Mowabu monga zitoliro, ndipo mtima wanga uwalirira anthu a Kiriheresi monga zitoliro, chifukwa chake zakuchuluka zake adadzionera zatayika. Pakuti mitu yonse ili yadazi, ndipo ndevu zili zosengedwa; pa manja onse pali pochekedwachekedwa, ndi pachiuno chiguduli. Pamwamba pa machindwi a Mowabu ndi m'miseu mwake muli kulira monsemonse; pakuti ndaswa Mowabu monga mbiya m'mene mulibe chikondwero, ati Yehova. Yasweka bwanji! Akuwa bwanji Mowabu! Wapotoloka bwanji ndi manyazi! Chomwecho Mowabu adzakhala choseketsa ndi choopsera onse omzungilira iye. Pakuti Yehova atero: Taonani, adzauluka ngati chiombankhanga, adzamtambasulira Mowabu mapiko ake. Keriyoti walandidwa, ndi malinga agwidwa, ndipo tsiku lomwelo mtima wa anthu amphamvu a Mowabu adzakhala ngati mtima wa mkazi alinkudwala. Ndipo Mowabu adzaonongeka asakhalenso mtundu wa anthu, chifukwa anadzikuzira yekha pa Yehova. Mantha, ndi dzenje, ndi khwekhwe, zili pa iwe, wokhala m'Mowabu, ati Yehova. Ndipo iye wakuthawa chifukwa cha mantha adzagwa m'dzenje; ndi iye amene atuluka m'dzenje adzagwidwa m'khwekhwe; pakuti ndidzatengera pa iye, pa Mowabu, chaka cha kulangidwa kwao, ati Yehova. Iwo amene anathawa aima opanda mphamvu pansi pamthunzi wa Hesiboni; pakuti moto watuluka m'Hesiboni, ndi malawi a moto m'kati mwa Sihoni, nadya ngodya ya Mowabu, ndi pakati pamtu pa ana a phokoso. Tsoka iwe, Mowabu! Anthu a Kemosi athedwa; pakuti ana ako amuna atengedwa ndende, ndi ana ako akazi atengedwa ndende. Koma ndidzabwezanso undende wa Mowabu masiku akumaliza, ati Yehova. Ziweruzo za Mowabu ndi zomwezi. Za ana a Amoni. Yehova atero: Kodi Israele alibe ana amuna? Alibe wolowa dzina? M'mwemo mfumu yao yalowa pa Gadi chifukwa chanji, ndi anthu ake akhala m'midzi mwake? Chifukwa chake, taonani, masiku afika, ati Yehova, Ine ndidzamveketsa mfuu ya nkhondo yomenyana ndi Raba wa ana a Amoni; ndipo adzasanduka muunda wabwinja, ndipo ana ake akazi adzatenthedwa ndi moto; pamenepo Israele adzalanda iwo amene adamlanda, ati Yehova. Kuwa, iwe Hesiboni, pakuti Ai wapasuka; lirani, inu ana akazi a Raba, muvale chiguduli; chitani maliro, thamangani kwina ndi kwina pamipanda; pakuti mfumu yao idzalowa m'ndende, ansembe ake ndi akulu ake pamodzi. Chifukwa chanji udzitamandira ndi zigwa, chigwa chako choyendamo madzi, iwe mwana wamkazi wobwerera m'mbuyo, amene anakhulupirira chuma chake, nati, Adza kwa ine ndani? Taona ndidzakutengera mantha, ati Ambuye, Yehova wa makamu, akuchokera kwa onse amene akuzungulira iwe; ndipo mudzaingitsidwa yense kulozera maso ake, ndipo palibe amene adzasonkhanitsa osochera. Koma pambuyo pake ndidzabwezanso undende wa ana a Amoni, ati Yehova. Za Edomu. Yehova wa makamu atero: Kodi m'Temani mulibenso nzeru? Kodi uphungu wawathera akuchenjera? Kodi nseru zao zatha psiti? Thawani inu, bwerani, khalani mwakuya, inu okhala m'Dedani; pakuti ndidzatengera pa iye tsoka la Esau, nthawi yoti ndidzamlanga iye. Akafika kwa inu akutchera mphesa, sadzasiya mphesa zokunkha? Akafika usiku akuba, adzaononga mpaka kutha? Pakuti ndamvula Esau, ndamvundukula, sadzatha kubisala; mbeu zake zaonongeka, ndi abale ake, ndi anansi ake, ndipo palibe iye. Siya ana ako amasiye, Ine ndidzawasunga; akazi ako amasiye andikhulupirire Ine. Pakuti Yehova atero: Taonani, iwo amene sanaweruzidwe kuti amwe chikho adzamwadi; kodi iwe ndiye amene adzakhala wosalangidwa konse? Sudzakhala wosalangidwa, koma udzamwadi. Pakuti ndalumbira, Pali Ine ati Yehova, kuti Bozira adzakhala chizizwitso, chitonzo, chopasuka, ndi chitemberero; ndipo midzi yake yonse idzakhala yopasuka chipasukire. Ndamva mthenga wa kwa Yehova, ndipo mthenga watumidwa mwa amitundu, wakuti, Sonkhanani, mumdzere, nimuukire nkhondo. Pakuti, taona, ndakuyesa iwe wamng'ono mwa amitundu, ndi wonyozedwa mwa anthu. Koma za kuopsa kwako, kunyada kwa mtima wako kunakunyenga iwe, wokhala m'mapanga a thanthwe, woumirira msanje wa chitunda, ngakhale usanja chisanja chako pamwamba penipeni ngati chiombankhanga, ndidzakutsitsa iwe kumeneko, ati Yehova. Ndipo Edomu adzakhala chizizwitso; ndipo yense wakupitapo adzazizwa, ndipo adzatsonyera zovuta zake zonse. Monga m'kupasuka kwa Sodomu ndi Gomora ndi midzi inzake, ati Yehova, munthu aliyense sadzakhala m'menemo, mwana wa munthu aliyense sadzagona m'menemo. Taona, wina adzakwerera mudzi wolimba ngati mkango wochokera ku Yordani wosefuka; koma dzidzidzi ndidzamthamangitsa amchokere; ndipo aliyense amene asankhidwa, ndidzamuika woyang'anira wake, pakuti wakunga Ine ndani? Adzandiikira nthawi ndani? Ndipo mbusa adzaima pamaso panga ndani? Chifukwa chake tamvani uphungu wa Yehova, umene waupangira pa Edomu; ndi zimene walingalirira okhala m'Temani, ndithu adzawakoka, ana ang'ono a zoweta; ndithu adzayesa busa lao bwinja pamodzi nao. Dziko lapansi linthunthumira ndi phokoso la kugwa kwao; pali mfuu, phokoso lake limveka pa Nyanja Yofiira. Taonani, adzafika nadzauluka ngati chiombankhanga, adzatambasulira Bozira mapiko ake, ndipo tsiku lomwemo mtima wa anthu amphamvu a Edomu adzakhala ngati mtima wa mkazi alinkudwala. Za Damasiko. Hamati ndi Aripadi ali ndi manyazi, chifukwa anamva malodza, asungunuka kunyanja, adera nkhawa osatha kukhala chete. Damasiko walefuka, atembenukira kuti athawe, kunthunthumira kwamgwira; zovuta ndi kulira zamgwira iye, ngati mkazi alimkudwala. Alekeranji kusiya mudzi wa chilemekezo, mudzi wa chikondwero changa? Chifukwa chake anyamata ake adzagwa m'miseu yake, ndipo anthu onse a nkhondo adzatontholetsedwa tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu. Ndipo Ine ndidzayatsa moto m'khoma la Damasiko, udzathetsa zinyumba za Benihadadi. Za Kedara, ndi za maufumu a Hazori, amene anawakantha Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni. Yehova atero: Ukani, kwerani ku Kedara, funkhani ana a ku m'mawa. Mahema ao ndi zoweta zao adzazilanda, adzadzitengera nsalu zochingira zao, ndi katundu wao yense, ndi ngamira zao; ndipo adzafuulira iwo, Mantha ponseponse. Thawani inu, yendani kutali, khalani mwakuya, Inu okhala m'Hazori, ati Yehova; pakuti Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anapangira uphungu pa inu, nakulingalirirani. Nyamukani, kwererani mtundu wokhala ndi mtendere, wokhala osadera nkhawa, ati Yehova, amene alibe zitseko ndi mapiringidzo, okhala pa okha. Ndipo ngamira zao zidzakhala zofunkha, ndi unyinji wa ng'ombe zao udzakhala wolanda; ndipo ndidzabalalitsira kumphepo zonse iwo amene ameta m'mbali mwa tsitsi lao; ndipo ndidzatenga tsoka lao kumbali zao zonse, ati Yehova. Ndipo Hazori adzakhala mokhalamo ankhandwe, bwinja lachikhalire; simudzakhalamo munthu, simudzagonamo mwana wa munthu. Mau a Yehova amene anafika kwa Yeremiya mneneri, onena za Elamu poyamba kulamulira Zedekiya mfumu ya Yuda, kuti, Yehova wa makamu atero: Taonani, ndidzathyola uta wa Elamu, ndiwo mtima wa mphamvu yao. Pa Elamu ndidzatengera mphepo zinai kumbali zinai za mlengalenga, ndidzamwaza iwo kumphepo zonsezo; ndipo sikudzakhala mtundu kumene opirikitsidwa a Elamu sadzafikako. Ndipo ndidzachititsa Elamu mantha pamaso pa amaliwongo ao, ndi pamaso pa iwo ofuna moyo wao; ndipo ndidzatengera choipa pa iwo, mkwiyo wanga waukali, ati Yehova; ndipo ndidzatumiza lupanga liwalondole, mpaka nditawatha; ndipo ndidzaika mpando wachifumu wanga m'Elamu, ndipo ndidzaononga pamenepo mfumu ndi akulu, ati Yehova. Koma padzaoneka masiku akutsiriza, kuti ndidzabwezanso undende wa Elamu, ati Yehova. Mau amene ananena Yehova za Babiloni, za dziko la Ababiloni, mwa Yeremiya mneneri. Lalikirani mwa amitundu, falikitsani, kwezani mbendera; falikitsani, musabise; munene, Babiloni wagwidwa, Beli wachitidwa manyazi, Merodaki wathyokathyoka, zosema zake zachitidwa manyazi, mafano ake athyokathyoka. Pakuti mtundu wa anthu udzatuluka kumpoto kudzamenyana naye, udzachititsa dziko lake bwinja, losakhalamo anthu; athawa, apita, anthu ndi nyama. Masiku omwewo, nthawi yomweyo, ati Yehova, ana a Israele adzadza, iwo ndi ana a Yuda; pamodzi adzayenda m'njira mwao alinkulira, nadzafuna Yehova Mulungu wao. Adzafunsira Ziyoni nkhope zao zilikuyang'ana kumeneko, ndi kuti, Tiyeni inu, dzilumikizeni kwa Yehova m'chipangano cha muyaya chimene sichidzaiwalika. Anthu anga anakhala nkhosa zotayika; abusa ao anazisokeretsa pa mapiri onyenga; achoka kuphiri kunka kuchitunda; aiwala malo ao akupuma. Onse amene anazipeza anazidya; adani ao anati, Sitipalamula mlandu, chifukwa iwo anachimwira Yehova, ndiye mokhalamo zolungama, Yehova, chiyembekezo cha atate ao. Thawani pakati pa Babiloni, tulukani m'dziko la Ababiloni, mukhale monga atonde patsogolo pa zoweta. Pakuti, taonani, ndidzabukitsa ndidzafikitsa kudzamenyana ndi Babiloni msonkhano wa mitundu yaikulu kuchokera kudziko la kumpoto; ndipo adzaguba pomenyana ndi iye; kumeneko Babiloni adzachotsedwa; mivi yao idzakhala ngati ya munthu wamaluli wamphamvu; yosabwera chabe. Ndipo Kasidi adzakhala chofunkha; onse amene amfunkhitsa iye adzakhuta, ati Yehova. Chifukwa mukondwa, chifukwa musekerera, inu amene mulanda cholowa changa, chifukwa muli onenepa monga ng'ombe yaikazi yoponda tirigu, ndi kulira ngati akavalo olimba; amai anu adzakhala ndi manyazi ambiri; amene anakubalani adzathedwa nzeru; taonani, adzakhala wapambuyo wa amitundu, chipululu, dziko louma, bwinja. Chifukwa cha mkwiyo wa Yehova sadzakhalamo anthu, koma padzakhala bwinja; onse akupita pa Babiloni adzadabwa, adzatsonyera pa zovuta zake zonse. Gubani ndi kuzungulira Babiloni kumenyana naye, inu nonse okoka uta; mumponyere iye, osaderera mivi; pakuti wachimwira Yehova. Mumfuulire iye pomzungulira iye; pakuti wagwira mwendo; malinga ake agwa; makoma ake agwetsedwa; pakuti ndi kubwezera chilango kwa Yehova; mumbwezere chilango; monga iye wachita mumchitire iye momwemo. Muwathe ofesa ku Babiloni, ndi iwo amene agwira chisenga nyengo ya masika; chifukwa cha lupanga losautsa adzatembenukira yense kwa anthu ake, nadzathawira yense ku dziko lake. Israele ndiye nkhosa yolowerera, mikango yampirikitsa, poyamba inamudya mfumu ya Asiriya; ndipo pomaliza Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni wathyola mafupa ake. Chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Taonani, ndidzalanga mfumu ya ku Babiloni ndi dziko lake, monga ndinalanga mfumu ya Asiriya. Ndipo ndidzabwezeranso Israele kubusa lake, ndipo adzadya pa Karimele ndi pa Basani, moyo wake nudzakhuta pa mapiri a Efuremu ndi m'Giliyadi. Masiku omwewo, nthawi yomweyo, ati Yehova, zoipa za Israele zidzafunidwa, koma zidzasoweka; ndi zochimwa za Yuda, koma sizidzapezeka; pakuti ndidzakhululukira iwo amene ndidzawasiya ngati chotsala. Kwera kukamenyana ndi dziko la Merataimu, ndi okhala m'Pekodi, ipha nuononge konse pambuyo pao, ati Yehova, chita monga mwa zonse ndinakuuza iwe. Phokoso la nkhondo lili m'dziko lino, ndi lakuononga kwakukulu. Nyundo ya dziko lonse yaduka ndi kuthyoka! Babiloni wasanduka bwinja pakati pa amitundu! Ndakutchera iwe msampha, ndi iwenso wagwidwa, iwe Babiloni, ndipo sunadziwa, wapezeka, ndiponso wagwidwa, chifukwa walimbana ndi Yehova. Yehova watsegula pa nyumba ya zida zake, ndipo watulutsa zida za mkwiyo wake; pakuti Ambuye Yehova wa makamu, ali ndi ntchito m'dziko la Ababiloni. Tadzani kudzamenyana ndi iye kuchokera ku malekezero ake, tsegulani pa nkhokwe zake; unjikani zake monga miyulu, mumuononge konse; pasatsale kanthu ka pa iye. Iphani ng'ombe zamphongo zake zonse; zitsikire kukaphedwa; tsoka iwo! Pakuti tsiku lao lafika, tsiku la kulanga kwao. Mau a iwo akuthawa akupulumuka m'dziko la Babiloni, kuti alalikire m'Ziyoni kubwezera chilango kwa Yehova Mulungu wathu, kubwezera chilango chifukwa cha Kachisi wake. Memezani amauta amenyane ndi Babiloni, onse amene akoka uta; mummangire iye zithando pomzungulira iye, asapulumuke mmodzi wake yense; mumbwezere iye monga mwa ntchito yake; monga mwa zonse wazichita, mumchitire iye; pakuti anamnyadira Yehova, Woyera wa Israele. Chifukwa chake anyamata ake adzagwa m'miseu yake, ndi anthu ankhondo ake onse adzatontholetsedwa tsiku lomwelo, ati Yehova. Taonani, nditsutsana nawe, wonyada iwe, ati Ambuye, Yehova wa makamu; pakuti tsiku lako lafika, nthawi imene ndidzakulanga iwe. Ndipo wonyadayo adzakhumudwa nadzagwa, ndipo palibe amene adzamuutsa iye; ndipo Ine ndidzayatsa moto m'midzi yake, ndipo udzatentha onse akumzungulira iye. Yehova wa makamu atero. Ana a Israele ndi ana a Yuda asautsidwa pamodzi; ndipo onse amene anawagwira ndende awagwiritsitsa; akana kuwamasula. Mombolo wao ngwa mphamvu; dzina lake Yehova wa makamu: adzawanenera mlandu wao ndithu; kuti apumutse dziko lapansi, nadzidzimutse okhala m'Babiloni. Lupanga lili pa Ababiloni, ati Yehova, pa okhala m'Babiloni, pa akulu ake, ndi pa anzeru ake. Lupanga lili pa amatukutuku, ndipo adzapusa; lupanga lili pa anthu olimba ake, ndipo adzaopa. Lupanga lili pa akavalo ao, ndi pa magaleta ao, ndi pa anthu onse osanganizidwa amene ali pakati pake, ndipo adzakhala ngati akazi; lupanga lili pa chuma chake, ndipo chidzalandidwa. Chilala chili pa madzi ake, ndipo adzaphwa; pakuti ndi dziko la mafano osema, ndipo ayaluka ndi kufuna zoopsa. Chifukwa chake zilombo za kuchipululu ndi mimbulu zidzakhalamo, ndi nthiwatiwa zidzakhala m'menemo; ndipo sadzakhalamo anthu konse; ndipo sadzakhalamo m'mibadwomibadwo. Monga muja Yehova anagwetsa Sodomu ndi Gomora ndi midzi inzake, ati Yehova; anthu sadzakhalamo, mwana wa munthu sadzagonamo. Taonani, anthu achokera kumpoto; ndiwo mtundu waukulu, ndipo maufumu ambiri adzaukitsidwa kuchokera ku malekezero a dziko lapansi. Agwira uta ndi nthungo; ali ankharwe, alibe chifundo; mau ao apokosera ngati nyanja, ndipo akwera akavalo, yense aguba monga munthu wa kunkhondo, kukamenyana ndi iwe, mwana wamkazi wa Babiloni. Mfumu ya ku Babiloni yamva mbiri yao, ndipo manja ake alefuka; wagwidwa ndi nkhawa, ndi zowawa zonga za mkazi alimkudwala. Taonani, mtundu uja adzakwerera mudzi wolimba ngati mkango wochokera ku Yordani wosefuka; koma dzidzidzi ndidzauthamangitsa umchokere, ndipo aliyense amene asankhidwa, ndidzamuika woyang'anira wake; pakuti wakunga Ine ndani? Adzandiikira nthawi ndani? Ndipo mbusa adzaima pamaso panga ndani? Chifukwa chake tamvani uphungu wa Yehova, umene waupangira pa Babiloni; ndi zimene walingirira dziko la Ababiloni; ndithu adzawakoka, ana ang'ono a zoweta; ndithu adzayesa busa lao bwinja pamodzi nao. Dziko lapansi linthunthumira, pa phokoso la kugwidwa kwa Babiloni, ndipo mfuu wamveka mwa amitundu. Yehova atero: Taonani, ndidzaukitsira Babiloni, ndi iwo okhala m'Lebi-kamai, mphepo yoononga. Ndipo ndidzatuma ku Babiloni alendo, amene adzampeta iye, amene adzataya zonse m'dziko lake, pakuti tsiku la chisauko adzamenyana ndi iye pomzungulira pake. Wauta asakoke uta wake, asadzikweze m'malaya ake achitsulo; musasiye anyamata ake; muononge ndithu khamu lake lonse. Ndipo adzagwa ophedwa m'dziko la Ababiloni, opyozedwa m'miseu yake. Pakuti Israele ndi Yuda sasiyidwa ndi Mulungu wao, ndiye Yehova wa makamu: ngakhale dziko lao ladzala ndi uchimo kuchimwira Woyera wa Israele. Thawani pakati pa Babiloni, yense apulumuke moyo wake; musathedwe m'choipa chake; pakuti ndi nthawi ya kubwezera chilango; Yehova adzambwezera iye mphotho yake. Babiloni wakhala chikho chagolide m'dzanja la Yehova, amene analedzeretsa dziko lonse lapansi; amitundu amwa vinyo wake; chifukwa chake amitundu ali ndi misala. Babiloni wagwa dzidzidzi naonongedwa; mumkuwire iye; mutengere zowawa zake vunguti, kapena angachire. Tikadachiritsa Babiloni koma sanachire; mumsiye iye, tipite tonse yense kudziko lake; pakuti chiweruziro chake chifikira kumwamba, chinyamulidwa mpaka kuthambo. Yehova watulutsa chilungamo chathu; tiyeni tilalikire m'Ziyoni ntchito ya Yehova Mulungu wathu. Nolani mivi; gwirani zolimba zikopa; Yehova waukitsa mtima wa mafumu a Amedi; chifukwa alingalirira Babiloni kuti amuononge; pakuti ndi kubwezera chilango kwa Yehova; kubwezera chilango chifukwa cha Kachisi wake. Muwakwezere mbendera makoma a Babiloni, mulimbikitse ulonda, muike alonda, mupangiretu olalira, pakuti Yehova waganiziratu ndi kuchita chomwe ananena za okhala m'Babiloni. Iwe wokhala pa madzi ambiri, wochuluka chuma, chimaliziro chako chafika, chilekezero cha kusirira kwako. Yehova wa makamu walumbira pa Iye mwini, kuti, Ndithu ndidzakudzaza iwe ndi anthu, monga ndi madzombe; ndipo adzakukwezera iwe mfuu. Iye analenga dziko lapansi ndi mphamvu yake, wakhazika dziko lapansi ndi nzeru yake, ndi luso anayala thambo; pamene Iye anena mau, pali unyinji wa madzi m'mwamba, ndipo akweretsa nkhungu ku malekezero a dziko lapansi, ayesa mphezi ya mvula, atulutsa mphepo ya m'nyumba za chuma zake. Anthu onse ali opulukira ndi opanda nzeru; wakusula golide achitidwa manyazi ndi fanizo lake losema; pakuti fanizo lake loyenga lili bodza, mulibe mpweya m'menemo. Ngwachabe, chiphamaso; nthawi ya kulangidwa kwao adzatayika. Gawo la Yakobo silifanafana ndi izo; pakuti Iye ndiye analenga zonse; Israele ndi mtundu wa cholowa chake, dzina lake ndi Yehova wa makamu. Iwe ndiwe chibonga changa ndi zida zanga za nkhondo; ndi iwe ndidzathyolathyola amitundu, ndi iwe ndidzaononga maufumu; ndi iwe ndidzathyolathyola kavalo ndi wokwera wake; ndi iwe ndidzathyolathyola galeta ndi iye wokweramo; ndi iwe ndidzathyolathyola mwamuna ndi mkazi; ndi iwe ndidzathyolathyola wokalamba ndi mnyamata; ndi iwe ndidzathyolathyola mnyamata ndi namwali; ndi iwe ndidzathyolathyola mbusa ndi zoweta zake; ndi iwe ndidzathyolathyola wakulima ndi goli la ng'ombe lake; ndi iwe ndidzathyolathyola akazembe ndi ziwanga. Ndipo ndidzabwezera Babiloni ndi okhala m'Kasidi zoipa zao zonse anazichita m'Ziyoni pamaso panu, ati Yehova. Taona, ndimenyana ndi iwe, iwe phiri lakuononga, ati Yehova, limene liononga dziko lonse; ndipo ndidzakutambasulira iwe dzanja langa, ndipo ndidzakugubuduza iwe kumatanthwe, ndipo ndidzakuyesa iwe phiri lotenthedwa. Ndipo sadzachotsa pa iwe mwala wa pangodya, kapena mwala wa pamaziko; koma udzakhala bwinja nthawi zonse, ati Yehova. Kwezani mbendera m'dziko, ombani lipenga mwa amitundu, konzerani amitundu amenyane naye, mummemezere maufumu a Ararati, Mini, ndi Asikenazi; muike nduna; amenyane naye; mukweretse akavalo ngati dzombe. Konzerani amitundu amenyane ndi iye, mafumu a Amedi, akazembe ake, ndi ziwanga zake zonse, ndi dziko lonse la ufumu wake. Dziko linthunthumira ndi kuphwetekedwa, pakuti zimene Yehova analingalirira Babiloni zilipobe, zoti ayese dziko la Babiloni bwinja lopanda wokhalamo. Olimba a ku Babiloni akana kumenyana, akhala m'malinga ao; mphamvu yao yalephera; akhala ngati akazi; nyumba zake zapsa ndi moto; akapichi ake athyoka. Wamtokoma mmodzi adzathamanga kukakomana ndi mnzake, ndi mthenga mmodzi kukomana ndi mnzake, kukauza mfumu ya ku Babiloni kuti mudzi wake wagwidwa ponsepo; pamadooko patsekedwa, pamatamanda a mabango patenthedwa ndi moto, ndi anthu a nkhondo aopa. Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Mwana wamkazi wa Babiloni akunga dwale pamene aliunda; patsala kanthawi kakang'ono, ndipo nthawi yamasika idzamfikira iye. Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni wandidya ine, wandiphwanya ine, wandiyesa ine ngati mbiya yopanda kanthu, wandimeza ngati ng'ona, wadzaza m'kamwa mwake ndi zotsekemera zanga, wanditaya ine. Wokhala m'Ziyoni adzati, Chiwawa anandichitira ine ndi thupi langa chikhale pa Babiloni; nadzati Yerusalemu, Mwazi wanga ukhale pa okhala m'Kasidi. Chifukwa chake Yehova atero: Taona, ndidzanenera iwe mlandu wako, ndidzawabwezera chilango chifukwa cha iwe; ndidzaphwetsa nyanja yake, ndidzaphwetsa chitsime chake. Ndipo Babiloni adzasanduka miunda, mokhala ankhandwe, chizizwitso, chotsonyetsa, wopanda okhalamo. Adzabangula pamodzi ngati misona ya mikango; adzachita nthulu ngati ana a mikango. Pamene atentha, ndidzakonza madyerero ao, ndidzawaledzeretsa, kuti asangalale, agone chigonere, asanyamuke, ati Yehova. Ndidzawagwetsa kuti aphedwe monga anaankhosa amphongo, ndi atonde. Sesaki wagwidwatu! Chimene dziko lonse lapansi linachitamanda chalandidwa dzidzidzi! Babiloni wakhalatu bwinja pakati pa amitundu! Nyanja yakwera kufikira ku Babiloni; wamira ndi mafunde ake aunyinji. Midzi yake yakhala bwinja, dziko louma, chipululu mosakhalamo anthu, mosapita mwana wa munthu aliyense. Ndipo Ine ndiweruza Beli m'Babiloni, ndipo ndidzatulutsa m'kamwa mwake chomwe wachimeza; ndipo amitundu sadzasonkhaniranso konse kwa iye; inde, khoma la Babiloni lidzagwa. Anthu anga, tulukani pakati pake, mudzipulumutse munthu yense ku mkwiyo waukali wa Yehova. Mtima wanu usalefuke, musaope chifukwa cha mbiri imene idzamveka m'dzikomu; pakuti mbiri idzafika chaka china, pambuyo pake chaka china mbiri ina, ndi chiwawa m'dziko, wolamulira kumenyana ndi wolamulira. Chifukwa chake, taonani, masiku alinkudza, amene ndidzaweruza mafano osemasema a Babiloni, ndipo dziko lake lonse lidzakhala ndi manyazi; ndipo ophedwa ake onse adzagwa pakati pake. Pamenepo kumwamba ndi dziko lapansi, ndi zonse zili m'menemo, zidzaimba mokondwerera Babiloni; pakuti akufunkha adzafika kwa iye kuchokera kumpoto, ati Yehova. Monga Babiloni wagwetsa ophedwa a Israele, momwemo pa Babiloni padzagwa ophedwa a dziko lonse. Inu amene mwapulumuka kulupanga, pitani inu musaime chiimire; mukumbukire Yehova kutali, Yerusalemu alowe m'mtima mwanu. Tili ndi manyazi, chifukwa tamva mnyozo; manyazi aphimba nkhope zathu; pakuti alendo alowa m'malo opatulika a nyumba ya Yehova. Chifukwa chake, taona, masiku alinkudza, ati Yehova, amene ndidzaweruza mafano ake; ndipo pa dziko lake lonse olasidwa adzabuula. Ngakhale Babiloni adzakwera kumwamba, ngakhale adzalimbitsa msanje wa mphamvu yake, koma kuchokera kwa Ine akufunkha adzafika kwa iye, ati Yehova. Mau akufuula ochokera ku Babiloni, ndi a chionongeko chachikulu ku dziko la Ababiloni! Pakuti Yehova afunkha Babiloni, aononga m'menemo mau akulu; ndipo mafunde ake adzakokoma ngati madzi ambiri, mau ao aphokosera; pakuti wakufunkha wafika kwa iye, kwa Babiloni, ndi anthu ake olimba agwidwa, mauta ao athyokathyoka, pakuti Yehova ndiye Mulungu wakubwezera, adzabwezera ndithu. Ndipo ndidzaledzeretsa akulu ake ndi anzeru ake, akazembe ake ndi ziwanga zake, ndi anthu ake olimba; ndipo adzagona chigonere, sadzanyamuka, ati Mfumu, dzina lake ndi Yehova wa makamu. Yehova wa makamu atero: Makoma otakata a Babiloni adzagwetsedwa ndithu, ndi zitseko zake zazitali zidzatenthedwa ndi moto; anthu adzagwirira ntchito chabe, ndi mitundu ya anthu idzagwirira moto, nidzatopa. Mau amene Yeremiya mneneri anauza Seraya mwana wa Neriya, mwana wa Maseiya, pamene iye ananka ndi Zedekiya mfumu ya Yuda ku Babiloni chaka chachinai cha ufumu wake. Ndipo Seraya anali kapitao wa chigono chake. Ndipo Yeremiya analemba m'buku choipa chonse chimene chidzafika pa Babiloni, mau onse awa olembedwa za Babiloni. Ndipo Yeremiya anati kwa Seraya, Pamene ufika ku Babiloni, samalira kuti uwerenge mau awa onse, nuti, Inu Yehova, mwanena za malo ano, kuti mudzawatha, kuti asakhalemo, ngakhale anthu ngakhale nyama, koma akhale bwinja nthawi za nthawi. Ndipo padzakhala, utatha kuwerenga buku ili, ulimange ndi mwala, nuliponye pakati pa Yufurate; nuti, Chomwecho adzamira Babiloni, sadzaukanso chifukwa cha choipa chimene ndidzamtengera iye; ndipo adzatopa. Mau a Yeremiya ndi omwewo. Zedekiya anali wa zaka makumi awiri kudza chimodzi pamene analowa ufumu wake; ndipo analamulira m'Yerusalemu zaka khumi kudza chimodzi; dzina la amake ndi Hamutala mwana wamkazi wa Yeremiya wa ku Libina. Ndipo iye anachita zoipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonse anazichita Yehoyakimu. Pakuti zonse zinachitika m'Yerusalemu ndi m'Yuda chifukwa cha mkwiyo wa Yehova, mpaka anawachotsa pamaso pake; ndipo Zedekiya anampandukira mfumu ya Babiloni. Ndipo panaoneka chaka chachisanu ndi chinai cha ufumu wake mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anafika, iye ndi nkhondo yake, kuti amenyane ndi Yerusalemu, ndipo anammangira zithando; ndipo anammangira malinga pozungulira pake. Ndipo mudzi unazingidwa mpaka chaka cha khumi ndi chimodzi cha mfumu Zedekiya. Mwezi wachinai, tsiku lachisanu ndi chinai la mwezi, njala inavuta m'mudzi, ndipo anthu a m'dziko analibe zakudya. Pamenepo anaboola mudzi, ndipo anathawa amuna onse a nkhondo, natuluka m'mudzi usiku pa njira ya kuchipata cha pakati pa makoma awiri, imene inali pa munda wa mfumu; Ababiloni alikumenyana ndi mudzi pozungulira pake, ndipo anapita njira ya kuchidikha. Koma nkhondo ya Ababiloni inamtsata mfumu, nimpeza Zedekiya m'zidikha za ku Yeriko; ndipo nkhondo yake yonse inambalalikira iye. Ndipo anamgwira iye, namtengera kwa mfumu ya ku Babiloni ku Ribula m'dziko la Hamati; ndipo iye anamweruza. Ndipo mfumu ya ku Babiloni inapha ana a Zedekiya pamaso pake; niphanso akulu onse a Yuda m'Ribula. Ndipo anakolowola maso a Zedekiya, ndipo mfumu ya ku Babiloni inammanga m'zigologolo, nimtengera ku Babiloni, nimuika m'ndende mpaka tsiku la kufa kwake. Mwezi wachisanu, tsiku lakhumi la mwezi, ndicho chaka chakhumi ndi chisanu ndi chinai cha Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, analowa m'Yerusalemu Nebuzaradani kapitao wa alonda, amene anaimirira pamaso pa mfumu ya ku Babiloni: ndipo anatentha nyumba ya Yehova ndi nyumba ya mfumu, ndi nyumba zonse za m'Yerusalemu, ngakhale zinyumba zazikulu zonse, anazitentha ndi moto. Ndipo nkhondo yonse ya Ababiloni, imene inali ndi kapitao wa alonda, inagumula makoma onse a Yerusalemu pomzungulira pake. Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga ndende anthu aumphawi, ndi anthu otsala amene anatsala m'mudzi, ndi amene anapandukira, kutsata mfumu ya ku Babiloni, ndi otsala a unyinjiwo. Koma Nebuzaradani kapitao wa alonda anasiya aumphawi a padziko akhale akulima mphesa ndi akulima m'minda. Ndi mizati yamkuwa imene inali m'nyumba ya Yehova, ndi zoikapo ndi thawale lamkuwa zimene zinali m'nyumba ya Yehova, Ababiloni anazithyolathyola, nanka nao mkuwa wake wonse ku Babiloni. Ndiponso miphika, ndi zoolera, ndi mbano zao, ndi mbale, ndi zipande, ndi zipangizo zonse zamkuwa zimene anatumikira nazo, anazichotsa. Ndi zikho, ndi zopalira moto, ndi mbale, ndi miphika, ndi zoikapo nyali, ndi zipande, ndi mitsuko; ndi golide, wa zija zagolide, ndi siliva, wa zija zasiliva, kapitao wa alonda anazichotsa. Nsanamira ziwirizo, thawale limodzilo, ndi ng'ombe zamkuwa zinali pansi pa zoikapo, zimene mfumu Solomoni anazipangira nyumba ya Yehova; mkuwa wa zipangizo zonsezi sanathe kuyesa kulemera kwake. Koma nsanamirazo, utali wake wa nsanamira ina unafikira mikono khumi mphambu isanu ndi itatu; ndi chingwe cha mikono khumi ndi iwiri chinaizinga; kuchindikira kwake kunali zala zinai; inali yagweregwere. Ndipo korona wamkuwa anali pamwamba pake; utali wake wa korona mmodzi unali wa mikono isanu, ndi sefa ndi makangaza pakorona pozungulira pake, onse amkuwa: nsanamira inzake yomwe inali nazo zonga zomwezi, ndi makangaza. Ndipo pambali pake panali makangaza makumi asanu ndi anai kudza asanu ndi limodzi; ndipo makangaza onse anali zana limodzi pamade pozungulira pake. Ndipo kapitao wa alonda anatenga Seraya wansembe wamkulu, ndi Zefaniya wansembe wachiwiri, ndi akudikira pakhomo atatu; ndipo m'mudzi anatenga kazembe amene anali woyang'anira anthu a nkhondo ndi amuna asanu ndi awiri a iwo akuona nkhope ya mfumu, amene anapezedwa m'mudzi; ndi mlembi wa kazembe wa nkhondo, amene akamemeza anthu a m'dziko; ndi amuna makamu asanu ndi limodzi a anthu a m'dziko, amene anapezedwa pakati pa mudzi. Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga iwo, nadza nao kwa mfumu ya ku Babiloni ku Ribula. Ndipo mfumu ya ku Babiloni anawakantha, nawapha pa Ribula m'dziko la Hamati. Chomwecho Yuda anatengedwa ndende kutuluka m'dziko lake. Amenewa ndi anthu amene Nebukadinezara anatenga ndende: chaka chachisanu ndi chiwiri, Ayuda zikwi zitatu kudza makumi awiri ndi atatu; chaka chakhumi ndi chisanu ndi chitatu cha Nebukadinezara iye anatenga ndende kuchokera m'Yerusalemu anthu mazana asanu ndi atatu kudza makumi atatu ndi awiri; chaka cha makumi awiri ndi zitatu cha Nebukadinezara Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga ndende Ayuda mazana asanu ndi awiri kudza makumi anai ndi asanu; anthu onse anali zikwi zinai kudza mazana asanu ndi limodzi. Ndipo panali chaka cha makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri cha undende wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi ndi iwiri, tsiku la makumi awiri ndi asanu la mwezi, Evili-Merodaki mfumu ya ku Babiloni anaweramutsa mutu wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, namtulutsa iye m'ndende; nanena naye bwino, naika mpando wake upose mipando ya mafumu amene anali naye m'Babiloni. Ndipo anapindula zovala zake za m'ndende, ndipo sanaleke kudya pamaso pake masiku onse a moyo wake. Koma phoso lake mfumu ya ku Babiloni sanaleke kumpatsa, phoso tsiku ndi tsiku gawo lake, mpaka tsiku la kufa kwake, masiku onse a moyo wake. Ha! Mudziwo unadzala anthu, ukhalatu pa wokha! Ukunga mkazi wamasiye! Waukuluwo mwa amitundu, kalonga wamkazi m'madera a dziko wasanduka wolamba! Uliralira usiku; misozi yake ili pa masaya ake; mwa onse amene anaukonda mulibe mmodzi wakuutonthoza: Mabwenzi ake onse auchitira ziwembu, asanduka adani ake. Yuda watengedwa ndende chifukwa cha msauko ndi ukapolo waukulu; akhala mwa amitundu, sapeza popuma; onse akumlondola anampeza pakati popsinjikiza. M'njira za Ziyoni mulira posoweka akudzera msonkhano; pa zipata zake zonse papasuka; ansembe ake onse ausa moyo; anamwali ake asautsidwa; iye mwini namva zowawa. Amaliwongo ake asanduka akulu ake, adani ake napindula; pakuti Yehova wamsautsa pochuluka zolakwa zake; ana ake ang'ono alowa m'ndende pamaso pa adani ake. Ulemu wake wonse wamchokera mwana wamkazi wa Ziyoni; akalonga ake asanduka nswala zosapeza busa, anayenda opanda mphamvu pamaso pa wompirikitsa. M'masiku a msauko wake ndi kusochera kwake Yerusalemu ukumbukira zokondweretsa zake zonse zachikhalire; pogwidwa anthu ake ndi mdaniyo popanda wakuupulumutsa, mdaniwo anamuona naseka mwachipongwe mabwinja ake. Yerusalemu wachimwa kwambiri; chifukwa chake wasanduka chinthu chonyansa; onse akuulemekeza aupeputsa, pakuti auona wamaliseche; inde, uusa moyo, nubwerera m'mbuyo. Udyo wake unali m'nsalu zake; sunakumbukira chitsiriziro chake; chifukwa chake watsika mozizwitsa; ulibe wakuutonthoza; taonani, Yehova, msauko wanga, pakuti mdaniyo wadzikuza yekha. Amaliwongo atambasulira manja ao pa zokondweretsa zake zonse; pakuti waona amitundu atalowa m'malo ake opatulika, amene munalamulira kuti asalowe mumsonkhano mwanu. Anthu ake onse ausa moyo nafunafuna mkate; ndi zokondweretsa zao agula zakudya kuti atsitsimutse moyo wao; taonani, Yehova, nimupenye; pakuti ndasanduka wonyansa. Kodi muyesa chimenechi chabe, nonsenu opita panjira? Penyani nimuone, kodi chilipo chisoni china ngati changachi amandimvetsa ine, chimene Yehova wandisautsa nacho tsiku la mkwiyo wake waukali? Anatumiza moto wochokera kumwamba kulowa m'mafupa anga, unawagonjetsa; watchera mapazi anga ukonde, wandibwezera m'mbuyo; wandipululutsa ndi kundilefula tsiku lonse. Goli la zolakwa zanga lamangidwa ndi dzanja lake; zalukidwa, zakwera pakhosi panga; iye wakhumudwitsa mphamvu yanga; Ambuye wandipereka m'manja mwao, sindithai kuwalaka. Ambuye wapepula ngwazi zanga zonse pakati panga; waitanira msonkhano pa ine kuti uphwanye anyamata anga, Ambuye wapondereza namwaliyo, mwana wamkazi wa Yuda, monga mopondera mphesa. Chifukwa cha zimenezi ndilira; diso langa, diso langatu likudza madzi: Pakuti wonditonthoza, wotsitsimutsa moyo wanga, anditalikira; ana anga asungulumwa, pakuti adaniwo apambana. Ziyoni atambasula manja ake, palibe wakumtonthoza; Yehova walamulira kuti omzungulira Yakobo akhale adani ake; Yerusalemu wasanduka chinthu chonyansa pakati pao. Yehova ali wolungama; pakuti ndapikisana ndi m'kamwa mwake; mumvetu, mitundu ya anthu nonsenu, nimuone chisoni changa; anamwali ndi anyamata anga atha kulowa m'ndende. Ndinaitana akundikondawo koma anandinyenga; ansembe ndi akulu anga anamwalira m'mudzimu, alikufunafuna zakudya zotsitsimutsa miyoyo yao. Onani, Yehova; pakuti ndavutika, m'kati mwanga mugwedezeka; mtima wanga wasanduka mwa ine; pakuti ndapikisana nanu ndithu; kunjako lupanga limangopha ana; m'nyumba muli imfa. Iwo anamva kuti ndiusa moyo, palibe wonditonthoza; adani anga onse atha kumva msauko wanga, nakondwera kuti mwatero ndinu; mudzafikitsa tsiku lija mwalitchula, ndipo iwowo adzanga ine. Zoipa zao zonse zidze pamaso panu, muwachitire monga mwandichitira ine chifukwa cha zolakwa zanga zonse, pakuti ndiusa moyo kwambiri, ndi kulefuka mtima wanga. Ambuye waphimbatu ndi mtambo mwana wamkazi wa Ziyoni, pomkwiyira! Wagwetsa pansi kuchokera kumwamba kukoma kwake kwa Israele; osakumbukira poponda mapazi ake tsiku la mkwiyo wake. Yehova wameza nyumba zonse za Yakobo osazichitira chisoni; wagumula malinga a mwana wamkazi wa Yuda mwa ukali wake; wawagwetsera pansi, waipitsa ufumuwo ndi akalonga ake. Pokwiya moopsa walikha nyanga zonse za Israele; wabweza m'mbuyo dzanja lake lamanja pamaso pa adaniwo, natentha Yakobo ngati moto wamalawi wonyambita mozungulira. Wathifula uta wake ngati mdani, waima ndi dzanja lake lamanja ngati mmaliwongo; wapha onse okondweretsa maso; watsanulira ukali wake ngati moto pa hema wa mwana wamkazi wa Ziyoni. Yehova wasanduka mdani, wameza Israele; wameza zinyumba zake zonse, wapasula malinga ake; nachulukitsira mwana wamkazi wa Yuda maliro ndi chibumo. Wachotsa mwamphamvu dindiro lake ngati la m'munda; waononga mosonkhanira mwake; Yehova waiwalitsa anthu msonkhano ndi Sabata m'Ziyoni; wanyoza mfumu ndi wansembe mokwiya mwaukali. Ambuye wataya guwa lake la nsembe, malo ake opatulika amnyansira; wapereka m'manja a adani ake makoma a zinyumba zake; iwo anaphokosera m'nyumba ya Yehova ngati tsiku la msonkhano. Yehova watsimikiza mtima kupasula linga la mwana wamkazi wa Ziyoni; watambalika chingwe, osabweza dzanja lake kuti lisaonongepo; waliritsa tchemba ndi linga; zilefuka pamodzi. Zipata zake zalowa pansi; waononga ndi kuthyola mipiringidzo yake; mfumu yake ndi akalonga ake ali pakati pa amitundu akusowa chilamulo; inde, aneneri ake samalandira masomphenya kwa Yehova. Akulu a mwana wamkazi wa Ziyoni akhala pansi natonthola; aponya fumbi pa mitu yao, anamangirira chiguduli m'chuuno mwao: Anamwali a ku Yerusalemu aweramitsa pansi mitu yao. Maso anga alefuka ndi misozi, m'kati mwanga mugwedezeka; chiwindi changa chagwa pansi chifukwa cha kupasula kwa mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga; chifukwa tiana ndi oyamwa akomoka m'makwalala a mudziwu. Amati kwa amao, Tirigu ndi vinyo ali kuti? Pokomoka iwo ngati olasidwa m'makwalala a mudziwu, potsanulidwa miyoyo yao pa zifuwa za amao. Ndikuchitire umboni wotani? Ndikuyerekeze ndi chiyani, mwana wamkazi wa Yerusalemu? Ndikulinganize ndi chiyani kuti ndikutonthoze, namwaliwe, mwana wamkazi wa Ziyoni? Popeza akula ngati nyanja; ndani angakuchize? Aneneri ako anakuonera masomphenya achabe ndi opusa; osawulula mphulupulu yako kuti abweze undende wako, koma anakuonera manenero achabe ndi opambutsa. Onse opita panjira akuombera manja: Atsonya, napukusira mitu yao pa mwana wamkazi wa Yerusalemu, nati, kodi uwu ndi mudzi wotchedwa wokongola, wangwiro, wokondweretsa dziko lonse? Adani ako onse ayasamira pa iwe, atsonya nakukuta mano, nati, Taumeza; ndithu ili ndi tsiku tinaliyembekezalo, talipeza, taliona. Yehova wachita chomwe analingalira; watsiriza mau ake, amene analamulira nthawi yakale; wagwetsa osachitira chisoni; wakondweretsa adani pa iwe, wakweza nyanga ya amaliwongo ako. Mtima wao unafuula kwa Ambuye, linga iwe la mwana wamkazi wa Ziyoni, igwe misozi ngati mtsinje usana ndi usiku; usapume kanthawi, asaleke mwana wa diso lako. Tauka, tafuula usiku, poyamba kulonda; tsanulira mtima wako ngati madzi pamaso pa Ambuye; takwezera maso ako kwa Iye, chifukwa cha moyo wa tiana tako, timene tilefuka ndi njala pa malekezero a makwalala onse. Onani Yehova, nimupenye, mwachitira ayani ichi? Kodi akazi adzadya zipatso zao, kunena ana amene anawalera wokha? Kodi wansembe ndi mneneri adzaphedwa m'malo opatulika a Ambuye? Wamng'ono ndi nkhalamba agona pansi m'makwalala; anamwali ndi anyamata anga agwa ndi lupanga; munawapha tsiku la mkwiyo wanu, munawagwaza osachitira chisoni. Mwaitana zondiopsa mozungulira ngati tsiku la msonkhano; panalibe wopulumuka ndi wotsala tsiku la mkwiyo wa Yehova; omwe ndinawaseweza ndi kuwalera, adaniwo anawatsiriza. Ine ndine munthuyu wakuona msauko ndi ndodo ya ukali wake. Wanditsogolera, nandiyendetsa mumdima, si m'kuunika ai. Zoonadi amandibwezerabwezera dzanja lake monditsutsa tsiku lonse. Wagugitsa thupi langa ndi khungu langa, nathyola mafupa anga. Wandimangira zithando za nkhondo, wandizinga ndi ulembe ndi mavuto. Wandikhalitsa mumdima ngati akufa kale. Wanditsekereza ndi guta, sindingatuluke; walemeretsa unyolo wanga. Inde, pofuula ine ndi kuitana andithandize amakaniza pemphero langa. Watsekereza njira zanga ndi miyala yosema, nakhotetsa mayendedwe anga. Andikhalira chilombo cholalira kapena mkango mobisalira. Wapambutsa njira zanga, nanding'amba; nandipululutsa. Wathifula uta wake, nandiyesa polozetsa muvi. Walasa impso zanga ndi mivi ya m'phodo mwake. Ndasanduka wondiseka mtundu wanga wonse, ndi nyimbo yao tsiku lonse. Wandidzaza ndi zowawa, wandikhutitsa chivumulo. Wathyolanso mano anga ndi tinsangalabwi, wandikuta ndi phulusa. Watalikitsanso moyo wanga ndi mtendere; ndinaiwala zabwino. Ndipo ndinati, Mphamvu yanga yatha, osayembekezanso kanthu kwa Yehova. Kumbukirani msauko wanga ndi kusochera kwanga, ndizo chivumulo ndi ndulu. Moyo wanga uzikumbukirabe nuwerama mwa ine. Ndili nacho chiyembekezo popeza ndilingalira ichi ndiyembekeza kanthu. Chifukwa chakusathedwa ife ndicho chifundo cha Yehova, pakuti chisoni chake sichileka, chioneka chatsopano m'mawa ndi m'mawa; mukhulupirika ndithu. Moyo wanga uti, Gawo langa ndiye Yehova; chifukwa chake ndidzakhulupirira. Yehova akhalira wabwino omlindirira, ndi moyo womfunafuna. Nkokoma kuti munthu ayembekeze ndi kulindirira modekha chipulumutso cha Yehova. Nkokoma kuti munthu asenze goli ali wamng'ono. Akhale pa yekha, natonthole, pakuti Mulungu wamsenzetsa ilo. Aike kamwa lake m'fumbi; kapena chilipo chiyembekezo. Atembenuzire wompanda tsaya lake, adzazidwe ndi chitonzo. Pakuti Yehova sadzataya kufikira nthawi zonse. Angakhale aliritsa, koma adzachitira chisoni monga mwa kuchuluka kwa zifundo zake. Pakuti samasautsa dala, ngakhale kumvetsa ana a anthu chisoni. Kupondereza andende onse a m'dziko, kupambutsa chiweruzo cha munthu pamaso pa Wam'mwambamwamba; kukhotetsa mlandu wa munthu, zonsezi Ambuye sazikonda. Ndani anganene, chonena chake ndi kuchitikadi, ngati Ambuye salamulira? Kodi m'kamwa mwa Wam'mwambamwamba simutuluka zovuta ndi zabwino? Kodi munthu wamoyo adandauliranji pokhala m'zochimwa zake? Tisanthule ntiyese njira zathu ntibwerenso kwa Yehova. Titukulire mitima yathu ndi manja athu omwe kwa Mulungu ali kumwamba. Ife tilakwa ndi kupikisana nanu, ndipo Inu simunatikhululukira. Mwadzikuta ndi mkwiyo ndi kutilondola, mwatipha osachitira chisoni. Mwadzikuta ndi mtambo kuti pemphero lathu lisapyolemo. Mwatiika pakati pa amitundu ngati zinyalala ndi za kudzala. Adani athu onse anatiyasamira. Mantha ndi dzenje zitifikira, ndi phokoso ndi chionongeko. M'diso mwanga mutsika mitsinje ya madzi chifukwa cha mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga woonongedwa. Diso langa lingotsanulira osaleka, osapumula, kufikira Yehova adzazolika kumwamba ndi kuona. Diso langa limvetsa moyo wanga zowawa chifukwa cha ana akazi onse a m'mudzi mwanga. Ondida opanda chifukwa anandiinga ngati mbalame; anaononga moyo wanga m'dzenje, naponya mwala pamwamba pa ine; madzi anayenda pamwamba pa mutu panga, ndinati, Ndalikhidwa. Ndinaitana dzina lanu, Yehova, ndili m'dzenje lapansi; munamva mau anga; musabise khutu lanu popuma ndi pofuula ine. Munayandikira tsiku la kukuitanani ine; munati, Usaope. Ambuye munanenera moyo wanga milandu yake; munaombola moyo wanga. Yehova, mwaona choipa anandichitiracho, mundiweruzire. Mwaona kubwezera kwao konse ndi zopangira zao zonse za pa ine. Mwamva chitonzo chao, Yehova, ndi zopangira zao zonse za pa ine, milomo ya akutsutsana nane ndi zolingalira zao za pa ine tsiku lonse. Taonani kukhala ndi kunyamuka kwao; ndine nyimbo yao. Mudzawabwezera chilango, Yehova, monga mwa machitidwe a manja ao. Muphimbe mtima wao ndi kuwatemberera; mudzawalondola mokwiya ndi kuwaononga pansi pa thambo la Yehova. Ha! Golide wagugadi; golide woona woposa wasandulika; miyala ya malo opatulika yakhuthulidwa pa malekezero a makwalala onse. Ana a Ziyoni a mtengo wapatali, olingana ndi golide woyengetsa, angoyesedwa ngati mbiya zadothi zozipanga manja a woumba. Angakhale ankhandwe amapatsa bere, nayamwitsa ana ao; koma mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga wasanduka wankhanza, ngati nthiwatiwa za m'chipululu. Lilime la mwana woyamwa limamatira kumalakalaka kwake ndi ludzu; ana ang'ono apempha mkate koma palibe wakuwanyemera. Omwe anadya zolongosoka angosiyidwa m'makwalala; omwe analeredwa navekedwa mlangali afungatira madzala. Pakuti mphulupulu ya mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga, ikula koposa tchimo la Sodomu, umene unapasuka m'kamphindi, anthu osauchitira kanthu. Omveka ake anakonzeka koposa chipale chofewa, nayera koposa mkaka, matupi ao anafiira koposa timiyala toti psu; maonekedwe ao ananga a safiro wa mtengo wapatali. Maonekedwe ao ada koposa makala, sazindikirika m'makwalala; khungu lao limamatira pa mafupa ao, lakhwinyata, lasanduka ngati ndodo. Ophedwa ndi lupanga amva bwino kupambana ophedwa ndi njala; pakuti amenewa angokwalika napyozedwa, posowa zipatso za m'munda. Manja a akazi achisoni anaphika ana aoao; anali chakudya chao poonongeka mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga. Yehova wakwaniritsa kuzaza kwake, watsanulira ukali wake; anayatsa moto m'Ziyoni, unanyambita maziko ake. Mafumu a dziko lapansi sanakhulupirire, ngakhale onse okhala kunja kuno, kuti adani ndi amaliwongo adzalowadi m'zipata za Yerusalemu. Ndicho chifukwa cha machimo a aneneri ndi mphulupulu za ansembe ake, amene anakhetsa mwazi wa olungama pakati pake. Asochera m'makwalala ngati akhungu, aipsidwa ndi mwazi; anthu sangakhudze zovala zao. Amafuula kwa iwo, Chokani, osakonzeka inu, chokani, chokani, musakhudze kanthu. Pothawa iwo ndi kusochera, anthu anati mwa amitundu, sadzagoneranso kuno. Mkwiyo wa Yehova unawalekanitsa, sadzawasamaliranso; iwo sanalemekeze ansembe, sanakomere mtima akulu. Maso athu athedwa, tikali ndi moyo, poyembekeza thandizo chabe; kudikira tinadikira mtundu wosatha kupulumutsa. Amalondola mapazi athu, sitingayende m'makwalala athu; chitsiriziro chathu chayandikira, masiku athu akwaniridwa; pakuti chitsiriziro chathu chafikadi. Otilondola anaposa ziombankhanga za m'mlengalenga m'liwiro lao, anatithamangitsa pamapiri natilalira m'chipululu. Wodzozedwa wa Yehova, ndiye mpweya wa m'mphuno mwathu, anagwidwa m'maenje ao; amene tinanena kuti, Tidzakhala m'mthunzi mwake pakati pa amitundu, kondwera nusangalale, mwana wamkazi wa Edomu, wokhala m'dziko la Uzi; chikho chidzapita ngakhale mwa iwenso; udzaledzera ndi kuvula zako. Mphulupulu yako yatha, mwana wamkazi wa Ziyoni, Yehova sadzakutenganso ndende; koma adzazonda mphulupulu yako, mwana wa mkazi wa Edomu, nadzavumbulutsa zochimwa zako. Yehova, kumbukirani chotigwerachi, penyani nimuone chitonzo chathu. Cholowa chathu chasanduka cha alendo, ndi nyumba zathu za achilendo. Ndife amasiye opanda atate, amai athu akunga akazi amasiye. Tinamwa madzi athu ndi ndalama, tiona nkhuni zathu pozigula. Otilondola atigwira pakhosi pathu, tatopa osaona popumira. Tinagwira mwendo Ejipito ndi Asiriya kuti tikhute zakudya. Atate athu anachimwa, kulibe iwo; ndipo tanyamula mphulupulu zao. Akapolo atilamulira; palibe wotipulumutsa m'dzanja lao. Timalowa m'zoopsa potenga zakudya zathu, chifukwa cha lupanga la m'chipululu. Khungu lathu lapserera ngati pamoto chifukwa cha kuwawa kwa njala. Anaipitsa akazi m'Ziyoni, ndi anamwali m'midzi ya Yuda. Anawapachika akalonga manja ao; sanalemekeze nkhope za akulu. Anyamata ananyamula mphero, ana nakhumudwa posenza nkhuni. Akulu adatha kuzipata, anyamata naleka nyimbo zao. Chimwemwe cha mtima wathu chalekeka, masewera athu asanduka maliro. Korona wagwa pamutu pathu; kalanga ife! Pakuti tinachimwa. Chifukwa cha ichi mtima wathu ufooka, chifukwa cha izi maso athu achita chimbuuzi; pa phiri la Ziyoni lopasukalo ankhandwe ayendapo. Inu, Yehova, mukhala chikhalire, ndi mpando wanu wachifumu ku mibadwomibadwo. Bwanji mutiiwala chiiwalire, ndi kutisiya masiku ambirimbiri. Mutitembenuzire kwa Inu, Yehova, ndipo tidzatembenuzidwadi, mukonzenso masiku athu ngati kale lija. Koma mwatikaniza konse, mwatikwiyira kopambana. Ndipo kunali chaka cha makumi atatu, mwezi wachinai, tsiku lachisanu la mwezi, pokhala ine pakati pa andende kumtsinje Kebara, kunatseguka kumwamba, ndipo ndinaona masomphenya a Mulungu. Tsiku lachisanu la mwezi, ndicho chaka chachisanu cha kutengedwa ndende mfumu Yehoyakini, anadzadi mau a Yehova kwa Ezekiele wansembe, mwana wa Buzi, m'dziko la Ababiloni kumtsinje Kebara; ndi pomwepo dzanja la Yehova lidamkhalira. Ndinapenya, ndipo taonani, mkuntho wa mphepo wochokera kumpoto, mtambo waukulu ndi moto wofukusika m'mwemo, ndi pozungulira pake padachita cheza, ndi m'kati mwake mudaoneka ngati chitsulo chakupsa m'kati mwa moto. Ndi m'kati mwake mudaoneka mafaniziro a zamoyo zinai. Ndipo maonekedwe ao ndiwo anafanana ndi munthu, ndi yense anali nazo nkhope zinai, ndi yense wa iwo anali nao mapiko anai. Ndi mapazi ao anali mapazi oongoka, ndi kumapazi ao kunanga kuphazi kwa mwanawang'ombe; ndipo ananyezimira ngati mawalidwe a mkuwa wowalitsidwa. Zinali naonso manja a munthu pansi pa mapiko ao pa mbali zao zinai; ndipo zinaizi zinali nazo nkhope zao ndi mapiko ao. Mapiko ao analumikizana; sizinatembenuka poyenda; chilichonse chinayenda ndi kulunjika kutsogoloko. Mafaniziro a nkhope zao zinali nayo nkhope ya munthu; ndi izi zinai zinali nayo nkhope ya mkango pa mbali ya kudzanja lamanja; ndi izi zinai zinali nayo nkhope ya ng'ombe pa mbali ya kudzanja lamanzere; izi zinai zinali nayonso nkhope ya chiombankhanga. Ndi nkhope zao ndi mapiko ao zinagawikana kumutu; chilichonse chinali nao mapiko awiri olumikizana, ndi awiri anaphimba thupi. Ndipo zinayenda, chilichonse chinalunjika kutsogolo kwake uko mzimu unafuna kumukako zinamuka, sizinatembenuka poyenda. Kunena za mafaniziro a zamoyozo, maonekedwe ao ananga makala amoto, monga maonekedwe a miyuni; motowo unayendayenda pakati pa zamoyozo, ndi motowo unachita cheza, ndi m'motomo mudatuluka mphezi. Ndipo zamoyozo zinathamanga ndi kubwerera, ngati maonekedwe a mphezi yong'anima. Ndipo pakupenyerera ine zamoyozo, taonani, njinga imodziimodzi yoponda pansi pafupi ndi zamoyozo pa nkhope zao zinai. Maonekedwe a njingazi ndi mapangidwe ao ananga mawalidwe a berulo; ndi izi zinai zinafanana mafaniziro ao; ndi maonekedwe ao ndi mapangidwe ao anali ngati njinga ziwiri zopingasitsana. Poyenda zinayenda kumbali zao zinai, zosatembenuka poyenda. Ndi mikombero yake inali yokuzika ndi yoopsa; ndi izi zinai zinali ndi mikombero yao yodzala ndi maso pozungulira pao. Ndipo poyenda zamoyozo, njingazi zinayenda pambali pao; ndipo ponyamuka pansi zamoyozo, njinga zinanyamuka. Kuli konse mzimu ukuti umuke, zinamuka komwe mzimu ukuti umuke; ndi njingazi zinanyamuka pambali pa izi; pakuti mzimu wa zamoyozo unali m'njingazo. Poyenda zija zinayenda izi, poima zija zinaima izo; ndipo ponyamuka pansi zija njingazi zinanyamuka pambali pa izi; pakuti mzimu wa zamoyozo unali mu njingazi. Ndi pa mitu ya zamoyozi panali chifaniziro cha thambo, monga mawalidwe a krustalo woopsa, loyalika pamwamba pamitu pao. Ndi pansi pa thambolo mapiko ao analunjikana, lina kulunjika kulinzake; chilichonse chinali nao mapiko awiri akuphimba matupi ao, chakuno ndi chauko. Ndipo pakuyenda izi ndinamva mkokomo wa mapiko ao, ngati mkokomo wa madzi aakulu, ngati mau a Wamphamvuyonse, phokoso lakusokosera ngati phokoso la ankhondo; pakuima zinagwetsa mapiko ao. Ndipo panamveka mau pamwamba pa thambolo linali pamwamba pa mitu yao; pakuima izi zinagwetsa mapiko ao. Ndi pamwamba pa thambolo linali pamitu pao panali chifaniziro cha mpando wachifumu, maonekedwe ake ngati mwala wa safiro; ndipo pa chifaniziro cha mpando wachifumu panali chifaniziro ngati maonekedwe ake a munthu wokhala pamwamba pake. Ndipo ndinapenya ngati chitsulo chakupsa, ngati maonekedwe ake a moto m'kati mwake pozungulira pake, kuyambira maonekedwe a m'chuuno mwake ndi kumwamba kwake; ndipo kuyambira maonekedwe a m'chuuno mwake ndi kunsi kwake ndinaona ngati maonekedwe ake a moto; ndi kunyezimira kudamzinga. Ngati maonekedwe a utawaleza uli m'mtambo tsiku la mvula, momwemo maonekedwe a kunyezimira kwake pozungulira pake. Ndiwo maonekedwe a chifaniziro cha ulemerero wa Yehova. Ndipo pakuchipenya ndinagwa nkhope pansi, ndipo ndinamva mau a wina wakunena. Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, khala chilili, ndipo ndidzanena nawe. Ndipo unandilowa mzimu pamene ananena nane, ndi kundiimika ndikhale chilili; ndipo ndinamumva Iye wakunena nane. Nati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, ndikutumizira kwa ana a Israele, kwa mitundu ya anthu opanduka, amene anapandukana nane; iwo ndi makolo ao anandilakwira mpaka lero lomwe. Ndipo anawa, ndiwo achipongwe ndi ouma mtima, ndikutumiza kwa iwo; ndipo ukanene nao, Atero Yehova Mulungu. Ndipo iwowa, ngakhale akamva kapena akaleka kumva, (pakuti ndiwo nyumba yopanduka,) koma adzadziwa kuti panali mneneri pakati pao. Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu iwe, usawaopa, kapena kuopa mau ao; ingakhale mitungwi ndi minga ikhala ndi iwe, nukhala pakati pa zinkhanira, usaopa mau ao kapena kuopsedwa ndi nkhope zao; pakuti ndiwo nyumba yopanduka. Ndipo ukanene nao mau anga, ngakhale akamva kapena akaleka kumva; pakuti iwo ndiwo opanduka. Koma iwe, wobadwa ndi munthu, tamvera ichi ndilikunena nawe; usakhale iwe wopanduka, ngati nyumba ija yopanduka; tsegula pakamwa pako, nudye chomwe ndikupatsa. Ndipo pakupenya ine ndinaona dzanja londitulutsira, ndipo taonani, mpukutu wa buku m'mwemo; naufunyulula pamaso panga; ndipo unalembedwa m'kati ndi kubwalo; munalembedwa m'mwemo nyimbo za maliro, ndi chisoni, ndi tsoka. Ndipo ananena nane, Wobadwa ndi munthu iwe, Idya chimene wachipeza; idya mpukutu uwu, numuke ndi kunena ndi nyumba ya Israele. Pamenepo ndinatsegula pakamwa panga ndipo anandidyetsa mpukutuwo. Nati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, dyetsa m'mimba mwako, nudzaze matumbo ako ndi mpukutu uwu ndakupatsawu. M'mwemo ndinaudya, ndi m'kamwa mwanga munazuna ngati uchi. Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, Muka, nufike kwa nyumba ya Israele, nunene nao mau anga. Pakuti sutumizidwa kwa anthu a chinenedwe chosamveka ndi chovuta, koma kwa nyumba ya Israele; si kwa mitundu yambiri ya anthu a chinenedwe chosamveka ndi chovuta, amene sukhoza kudziwitsa chinenedwe chao. Zedi ndikakutumiza kwa iwowa adzamvera iwe. Koma nyumba ya Israele siidzakumvera, pakuti siifuna kundimvera Ine; pakuti nyumba yonse ya Israele ndiyo yolimba mutu ndi youma mtima. Taona ndakhwimitsa nkhope yako itsutsane nazo nkhope zao; ndalimbitsanso mutu wako utsutsane nayo mitu yao. Ndalimbitsa mutu wako woposa mwala wolimbitsitsa, usawaopa kapena kutenga nkhawa pamaso pao; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka. Ananenanso nane, Wobadwa ndi munthu iwe, mau anga onse ndidzawanena ndi iwe uwalandire m'mtima mwako, utawamva m'makutu mwako. Numuke, nufike kwa andende kwa ana a anthu a mtundu wako, nunene nao ndi kuwauza, Atero Yehova Mulungu, ngakhale akamva kapena akaleka kumva. Pamenepo mzimu unandinyamula, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau a mkokomo waukulu, ndi kuti, Wodala ulemerero wa Yehova m'malo mwake. Ndipo ndinamva mkokomo wa mapiko a zamoyozo pakukhudzana, ndi mlikiti wa njingazo m'mbali mwa izo, ndilo phokoso la mkokomo waukulu. M'mwemo mzimu unandinyamula ndi kuchoka nane; ndipo ndinamuka wowawidwa, womyuka mtima; koma dzanja la Yehova linandigwirizitsa. Ndipo ndinafika kwa andende ku Telabibu, okhala kumtsinje Kebara, ndiko kwao; ndipo ndinakhalako wodabwa pakati pao masiku asanu ndi awiri. Ndipo kunali atatha masiku asanu ndi awiri, mau a Yehova anandidzera, ndi kuti, Wobadwa ndi munthu iwe, ndakuika ukhale mlonda wa nyumba ya Israele, m'mwemo mvera mau otuluka m'kamwa mwanga, nundichenjezere iwo. Ndikanena kwa woipa, Udzafa ndithu, koma iwe osamchenjeza, wosanena kumchenjeza woipayo aleke njira yake yoipa, kumsunga ndi moyo, woipa yemweyo adzafa mu mphulupulu yake; koma mwazi wake ndidzaufuna pa dzanja lako. Koma ukachenjeza woipa, osabwerera iye kuleka choipa chake kapena njira yake yoipa, adzafa mu mphulupulu yake; koma iwe walanditsa moyo wako. Momwemonso akabwerera wolungama kuleka chilungamo chake, ndi kuchita chosalungama, ndipo ndikamuikira chomkhumudwitsa, adzafa; popeza sunamchenjeza, adzafa m'tchimo lake, ndi zolungama zake adazichita sizidzakumbukika; koma mwazi wake ndidzaufuna pa dzanja lako. Koma ukamchenjeza wolungamayo, kuti asachimwe wolungamayo, ndipo sachimwa, adzakhala ndi moyo ndithu, popeza anachenjezedwa; ndipo iwe walanditsa moyo wako. Ndipo dzanja la Yehova linandikhalira komweko, nati kwa ine, Nyamuka, tuluka kunka kuchidikha, ndipo pomwepo ndidzalankhula ndi iwe. Ndipo ndinauka ndi kutuluka kunka kuchidikha, ndipo taonani, ulemerero wa Yehova unaimako monga ulemerero uja ndinauona kumtsinje Kebara, ndipo ndinagwa nkhope pansi. Pamenepo unandilowa mzimu ndi kundiimika ndikhale chilili; ndipo analankhula ndi ine, nanena nane, Muka, katsekedwe m'nyumba mwako. Koma iwe wobadwa ndi munthu, taona, adzakuikira iwe zingwe zolimba, nadzakumanga nazo, ndipo sudzatuluka pakati pao; ndipo ndidzamamatiritsa lilime lako kumalakalaka ako, kuti ukhale wosanena, wosawakhalira wakuwadzudzula; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka. Koma pamene ndilankhula nawe ndidzatsegula pakamwa pako, nudzanena nao, Atero Yehova Mulungu. Wakumvera amvere, wosafuna kumvera akhale; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka. Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, dzitengere njerwa, nuiike pamaso pako, nulembepo mudzi, ndiwo Yerusalemu; nuuzinge, nuumangire nsanja zouzinga, nuundire nthumbira, ndi kuumangira misasa, nuuikire zogumulira pozungulira pake. Nudzitengere chiwaya chachitsulo, ndi kuchiika ngati khoma lachitsulo pakati pa iwe ndi mudziwo; nuulozetsere nkhope yako kuti umangidwire misasa, ndipo udzamangira misasa. Ichi chikhale chizindikiro cha nyumba ya Israele. Ndipo iwe ugonere pansi mbali yako ya kumanzere, nuikepo mphulupulu ya nyumba ya Israele; monga mwa kuwerenga kwa masiku amene udzagonapo udzasenza mphulupulu yao. Ndipo Ine ndakuikira zaka za mphulupulu yao ngati masiku, ndiwo masiku mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai, kuti usenze mphulupulu ya nyumba ya Israele. Ndipo utatsiriza awa, ugonerenso mbali yako ya kumanja, ndi kusenza mphulupulu ya nyumba ya Yuda; ndakuikira masiku makumi anai, kuliyesa tsiku limodzi ngati chaka chimodzi. Ndipo ulozetse nkhope yako kuzingidwa kwake kwa Yerusalemu, ndi dzanja lako losafundika, nuunenere. Ndipo taona ndidzakumanga ndi zingwe zolimba kuti usakunkhulire, mpaka watsiriza masiku a kuzingidwa kwako. Udzitengerenso tirigu, ndi barele, ndi nyemba, ndi mphodza, ndi mapira, ndi mawere, nuziike m'mbale imodzi, ndi kudzipangira mkate nazo; uzidyako monga mwa kuwerenga kwa masiku udzagonawo pambali pako, ndiwo masiku mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai, Ndipo chakudya chako uzichidya chiyesedwe masekeli makumi awiri tsiku limodzi; uzidyako tsiku ndi tsiku pa nthawi yake. Uzimwanso madzi monga mwa muyeso, limodzi la magawo asanu ndi limodzi la hini; uzimwako tsiku ndi tsiku pa nthawi yake. Ndipo uzichidya ngati timikate ta barele, ndi kutiocha pamaso pao ndi zonyansa za munthu. Ndipo Yehova anati, Motero ana a Israele adzadya chakudya chao chodetsedwa, mwa amitundu kumene ndidzawaingitsirako. Pamenepo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! Taonani, moyo wanga sunadetsedwa, pakuti chiyambire ubwana wanga mpaka tsopano sindinadye chinthu chakufa chokha, kapena chogwidwa ndi chilombo; simunalowanso m'kamwa mwanga nyama yonyansa. Ndipo anati kwa ine, Taona ndakuninkha ndowe ya ng'ombe m'malo mwa zonyansa za munthu, uotche mkate wako pamenepo. Nanenanso nane, Wobadwa ndi munthu iwe, taona, ndidzathyola mchirikizo, ndiwo chakudya, m'Yerusalemu; ndipo adzadya chakudyacho monga mwa muyeso, ndi mosamalira, nadzamwa madzi monga mwa muyeso, ndi kudabwa; kuti asowe chakudya ndi madzi, nasumwesumwe, naondetse mu mphulupulu zao. Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, udzitengere mpeni wakuthwa, ndiwo lumo la wometa, udzitengere ndi kulipititsa pamutu pako ndi pa ndevu zako; nudzitengere muyeso kuyesa nao, ndi kugawa tsitsilo. Limodzi la magawo ake atatu utenthe ndi moto pakati pa mudzi pakutha masiku a kuzingidwa mudzi, nutenge gawo lina ndi kukwapulakwapula ndi lupanga pozungulira pake, nuwaze kumphepo gawo lotsala; pakuti ndidzasolola lupanga lakuwatsata. Utengekonso owerengeka ndi kuwamanga m'mkawo wa malaya ako. Nutengekonso pa amenewa ndi kuwaponya pakati pa moto, ndi kuwatentha m'moto; kuchokera kumeneko udzatuluka moto pa nyumba yonse ya Israele. Atero Yehova Mulungu, Uwu ndi Yerusalemu ndinauika pakati pa amitundu, ndi pozungulira pake pali maiko. Koma anakaniza maweruzo anga ndi kuchita zoipa zoposa amitundu, nakaniza malemba anga koposa maiko akuzungulira; pakuti anataya maweruzo anga, ndi malemba anga, sanayendemo. Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza kupokosera kwanu kwaposa kwa amitundu akukuzingani, ndipo simunayenda m'malemba anga, kapena kuchita maweruzo anga, ngakhale maweruzo a amitundu akukuzingani simunawachita; chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona ndidzatsutsana nawe Inedi, ndi kuchita maweruzo pakati pako pamaso pa amitundu. Ndipo ndidzachita mwa iwe chimene sindinachichita ndi kale lonse, ndi kusadzachitanso momwemo, chifukwa cha zonyansa zako zonse. Chifukwa chake atate adzadya ana pakati pako, ndi ana adzadya atate ao; ndipo ndidzachita maweruzo mwa iwe, ndi akutsala onse ndidzawabalalitsa kumphepo zonse. M'mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, popeza wadetsa malo anga opatulika ndi zonyansa zako zonse ndi zoipsa zako zonse, ndidzakuchepsa; diso langa silidzalekerera, ndi Inenso sindidzachita chifundo. Limodzi la magawo atatu la iwe lidzafa ndi mliri, nilidzatha ndi njala pakati pa iwe; ndi limodzi lidzagwa ndi lupanga pozinga pako; ndi limodzi ndidzalibalalikitsa kumphepo zonse, ndi kuwasololera lupanga lakuwatsata. Motero mkwiyo wanga udzakwaniridwa, ndipo ndidzakhutitsa ukali wanga pa iwo, ndi kudzitonthoza; ndipo adzadziwa kuti Ine Yehova ndinanena m'changu changa, pokwaniridwa nao ukali wanga. Ndidzakuikanso ukhale bwinja ndi chotonza pakati pa amitundu akukuzinga, pamaso pa onse akupitirirapo. Momwemo chidzakhala chotonza ndi mnyozo, chilangizo ndi chodabwitsa kwa amitundu akukuzinga, pamene ndikuchitira maweruzo mu mkwiyo ndi ukali ndi madzudzulo aukali; Ine Yehova ndanena. Pakuwatumizira Ine mivi yoipa ya njala yakuononga, imene ndidzatumiza kukuonongani, pamenepo ndidzakukuzirani njala, ndi kukuthyolerani mchirikizo, ndiwo chakudya. Inde ndidzakutumizirani njala ndi zilombo, ndipo zidzakusowetsa ana ako; ndi mliri ndi mwazi zidzakugwera; ndidzakufikitsiranso lupanga; Ine Yehova ndachinena. Ndipo mau a Yehova anandidzera, kuti, Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako kumapiri a Israele, uwanenere, nunene, Mapiri a Israele inu, tamverani mau a Yehova Mulungu: Atero Yehova Mulungu kwa mapiri ndi zitunda, kwa mitsinje ndi zigwa, Taonani, Ine ndikufikitsirani lupanga, ndipo ndidzaononga misanje yanu. Ndi maguwa anu a nsembe adzakhala opasuka, ndi zoimiritsa zanu zadzuwa zidzasweka; ndipo ndidzagwetsa ophedwa anu pamaso pa mafano anu. Ndipo ndidzaika mitembo ya ana a Israele pamaso pa mafano anu, ndi kumwaza mafupa anu mozungulira maguwa anu a nsembe. Pokhala inu ponse midzi idzapasuka, ndi misanje idzakhala yabwinja; kuti maguwa anu a nsembe akhale opasuka ndi mabwinja, ndi mafano anu asweke nalekeke, ndi zoimiritsa zanu zadzuwa zilikhidwe, ndi ntchito zanu zifafanizidwe. Ndi ophedwa adzagwa pakati panu, motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Koma ndidzasiyapo otsala, popeza mudzakhala nao ena akupulumuka lupanga mwa amitundu pobalalitsidwa inu m'maiko maiko. Pamenepo akupulumuka anu adzandikumbukira Ine kwa amitundu kumene anatengedwa ndende, kuti ndasweka ndi mtima wao wachigololo wolekana ndi Ine, ndi maso ao achigololo akutsata mafano ao; ndipo iwo adzakhala onyansa pamaso pao pa iwo eni, chifukwa cha zoipa anazichita m'zonyansa zao zonse. Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, sindinanena chabe kuti ndidzawachitira choipa ichi. Atero Yehova Mulungu, Omba manja ako, ponda ndi phazi lako, nuti, Kalanga ine, chifukwa cha zonyansa zoipa zonse za nyumba ya Israele; pakuti adzagwa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri. Wokhala kutali adzafa ndi mliri, wokhala pafupi adzagwa ndi lupanga; koma wotsala ndi kuzingidwa adzafa ndi njala; momwemo ndidzawakwaniritsira ukali wanga. Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pokhala ophedwa ao pakati pa mafano ao, pozinga maguwa ao a nsembe, pa zitunda zonse zazitali, pamwamba pa mapiri onse, ndi patsinde pa mitengo yogudira yonse, ndi patsinde pa thundu aliyense wagudugudu, pomwe adapereka zonunkhira zokoma kwa mafano ao onse. Ndipo ndidzawatambasulira dzanja langa, ndi kulisandutsa dziko bwinja ndi lopasuka, koposa chipululu cha ku Ribula mokhalamo iwo monse; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Ndipo mau a Yehova anandidzera, akuti, Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, atero Ambuye Yehova kwa dziko la Israele, Kwatha; kwafika kutha kwake pangodya zinai za dziko. Tsopano kwakudzera kutha kwako, ndipo ndidzakutumizira mkwiyo wanga, ndi kukuweruza monga mwa njira zako, ndipo ndidzakubwezera zonyansa zako zonse. Ndipo diso langa silidzakulekerera, sindidzachita chifundo, koma ndidzakubwezera njira zako, ndi zonyansa zako zidzakhala pakati pako; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Atero Yehova Mulungu, Choipa, choipa cha pa chokha, taona chilinkudza. Kutha kwafika, kwafika kutha. Kwakugalamukira, taona kwafika. Tsoka lako lakufikira, nzika iwe, yafika nthawi, tsiku lili pafupi, ndilo laphokoso, si lakufuula mokondwera kumapiri. Katsala kamphindi, ndipo ndidzakutsanulira ukali wanga, ndi kukukwaniritsira mkwiyo wanga, ndi kukuweruza monga mwa njira zako, ndipo ndidzakubwezera zonyansa zako zonse. Ndipo diso langa silidzalekerera, wosachita chifundo Ine, ndidzakubwezera monga mwa njira zako, ndi zonyansa zako zidzakhala pakati pako; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova wakukantha. Taona, tsikuli, taona, lafika; tsoka lako latuluka, ndodo yaphuka mphundu za maluwa, kudzitama kwaphuka. Chiwawa chauka chikhale ndodo ya choipa; sadzawatsalira ndi mmodzi yense, kapena wa unyinji wao, kapena wa chuma chao; sipadzakhalanso kuwalira maliro. Yafika nthawi, layandikira tsikulo, wogula asakondwere, ndi wogulitsa asamve chisoni; pakuti mkwiyo ukhalira unyinji wao wonse. Pakuti wogulitsa sadzabwera ku chogulitsacho, chinkana akali ndi moyo, popeza masomphenyawo akunena unyinji wake wonse sadzapita pachabe, ndipo palibe mmodzi adzalimbitsa moyo wake m'mphulupulu yake. Aomba lipenga, nakonzeratu zonse, koma palibe womuka kunkhondo; pakuti mkwiyo wanga ukhalira unyinji wake wonse. Kunja kuli lupanga, ndi m'katimo muli mliri ndi njala; wokhala kuthengo adzafa ndi lupanga, ndi wokhala m'mudziyo njala ndi mliri zidzamutha. Ndipo akupulumuka mwa iwo adzapulumuka, koma adzakhala kumapiri ngati njiwa za kuzigwa, onse akubuula, aliyense m'mphulupulu zake. Manja onse adzalenda, ndi maondo onse adzaweyeseka ngati madzi. Ndipo adzadzimangira m'chuuno ndi ziguduli, ndi zoopsetsa zidzawaphimba, ndi nkhope zonse zidzachita manyazi, ndi mitu yao yonse idzachita dazi. Adzataya siliva wao kumakwalala, nadzayesa golide wao chinthu chodetsedwa; siliva wao ndi golide wao sadzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova, sadzakwaniritsa moyo wao, kapena kudzaza matumbo ao; pakuti izi ndi chokhumudwitsa cha mphulupulu zao. Ndipo chokometsera chake chokongola anachiyesa chodzikuza nacho, napangira mafanizo olaula, ndi zonyansa zao zina; chifukwa chake ndinapatsa ichi chikhale chowadetsa. Ndipo ndidzachipereka m'dzanja la alendo chikhale cholandika, ndi kwa oipa a m'dziko chikhale chofunkha; ndipo adzachiipsa. Ndipo nkhope yanga idzawayang'anira kumbali, ndipo iwo adzadetsa pobisika panga, nadzalowamo achifwamba, nadzamudetsa. Sula unyolo, popeza dziko ladzala ndi milandu yamwazi, ndi mudzi wadzala ndi chiwawa. Chifukwa chake ndidzabwera nao amitundu oipitsitsa, ndipo iwo adzalandira nyumba zao ngati cholowa, ndidzaleketsanso kudzikuza kwa amphamvu, kuti adetsedwe malo ao opatulika. Chionongeko chilinkudza, adzafunafuna mtendere, koma palibe. Lidzafika tsoka lotsatanatsatana, kudzakhalanso mbiri yotsatanatsatana, ndipo adzafunafuna masomphenya a mneneri, koma malamulo adzatayikira wansembe, uphungu ndi kutayikira akulu. Mfumu idzalira maliro, ndi kalonga adzavala chipasuko, ndi manja a anthu a m'dziko adzanjenjemera. Ndidzawachitira monga mwa njira zao, ndi kuwaweruza monga mwa maweruzo ao; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Ndipo kunali chaka chachisanu ndi chimodzi, mwezi wachisanu ndi chimodzi, tsiku lachisanu la mweziwo, pokhala ine m'nyumba mwanga, akulu a Yuda omwe analikukhala pamaso panga, dzanja la Yehova Mulungu linandigwera komweko. Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, chifaniziro cha maonekedwe a moto; kuyambira maonekedwe a m'chuuno mwake ndi kunsi kwake, moto; ndi kuyambira m'chuuno mwake ndi kumwamba kwake, monga maonekedwe a cheza, ngati chitsulo chakupsa. Ndipo anatambasula chonga dzanja, nandigwira tsitsi la pamutu panga; ndipo mzimu unandilengetsa pakati pa dziko ndi thambo, numuka nane m'masomphenya a Mulungu ku Yerusalemu, ku chitseko cha chipata cha bwalo la m'katimo loloza kumpoto, kumene kunali mpando wa fano la nsanje lochititsa nsanje. Ndipo taonani, pomwepo panali ulemerero wa Mulungu wa Israele, monga mwa maonekedwe ndinawaona kuchidikha chija. Pamenepo ananena ndi ine, Wobadwa ndi munthu iwe, kweza maso ako kunjira yoloza kumpoto. Ndipo ndinakweza maso anga kunjira yoloza kumpoto, ndipo taonani, kumpoto kwa chipata cha guwa la nsembe fano ili la nsanje polowera pake. Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, uona kodi izi alikuzichita? Zonyansa zazikulu nyumba ya Israele ilikuzichita kuno, kuti ndichoke kutali kwa malo anga opatulika? Koma udzaonanso zonyansa zina zoposa. Ndipo anadza nane kuchipata cha kubwalo, ndipo popenya ine, taonani, pobooka palinga. Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, booletsa kulinga; ndipo nditabooletsa palinga, ndinaona khomo. Ndipo anati kwa ine, Lowa, kapenye zonyansa zoipa alikuzichita komweko. M'mwemo ndinalowa ndi kupenya, ndipo taonani, maonekedwe ali onse a zokwawa, ndi zilombo zonyansa, ndi mafano onse a nyumba ya Israele, zolembedwa pakhoma pozungulira ponse. Ndipo pamaso pao panaima amuna makumi asanu ndi awiri a akulu a nyumba ya Israele, ndi pakati pao panaima Yazaniya mwana wa Safani, munthu aliyense ndi mbale yake ya zofukiza m'dzanja lake; ndi fungo lake la mtambo wa zonunkhira linakwera. Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, wapenya kodi chochita akulu a nyumba ya Israele mumdima, aliyense m'chipinda chake cha zifanizo? Pakuti ati, Yehova satipenya, Yehova wataya dziko. Anatinso kwa ine, Udzaonanso zonyansa zazikulu zina azichita. Pamenepo anadza nane kuchitseko cha chipata cha nyumba ya Yehova choloza kumpoto; ndipo taonani, apo panakhala akazi akulirira Tamuzi. Ndipo anati kwa ine, Wachiona ichi, wobadwa ndi munthu iwe? Udzaonanso zonyansa zazikulu zoposa izi. Ndipo anadza nane ku bwalo lam'kati la nyumba ya Yehova, ndipo taonani, pa khomo la Kachisi wa Yehova, pakati pa khonde lake ndi guwa la nsembe, panali amuna ngati makumi awiri mphambu asanu akufulatira, ku Kachisi wa Yehova, ndi kuyang'ana kum'mawa, napembedza dzuwa kum'mawa. Ndipo anati kwa ine, Wachiona ichi, wobadwa ndi munthu iwe? Chinthu chopepuka ichi kodi ndi nyumba ya Yuda, kuti achite zonyansa azichita kunozi? Pakuti anadzaza dziko ndi chiwawa, nabwereranso kuutsa mkwiyo wanga, ndipo taonani, aika nthambi kumphuno kwao. Chifukwa chake Inenso ndidzachita mwaukali; diso langa silidzalekerera, osawachitira chifundo Ine; ndipo chinkana afuula m'makutu mwanga ndi mau akulu, koma sindidzawamvera Ine. Pamenepo Iye anafuula m'makutu mwanga ndi mau akulu, ndi kuti, Asendere oyang'anira mudzi, aliyense ndi chida chake choonongera m'dzanja lake. Ndipo taonani, anadza amuna asanu ndi mmodzi, odzera njira ya chipata cha kumtunda choloza kumpoto, aliyense ndi chida chake chophera m'dzanja lake; ndi munthu mmodzi pakati pao wovala bafuta, ndi zolembera nazo m'chuuno mwake. Ndipo analowa, naima m'mphepete mwa guwa la nsembe lamkuwa. Ndipo ulemerero wa Mulungu wa Israele unakwera kuchoka pa kerubi, pamene unakhalira kunka kuchiundo cha nyumba, naitana munthu wovala bafutayo wokhala ndi zolembera nazo m'chuuno mwake. Ndipo Yehova ananena naye, Pita pakati pa mudzi, pakati pa Yerusalemu, nulembe chizindikiro pa mphumi zao za anthu akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse zichitidwa pakati pake. Nati kwa enawo, ndilikumva ine, Pitani pakati pa mudzi kumtsata iye, ndi kukantha; maso anu asalekerere, musachite chifundo; iphanitu nkhalamba, mnyamata ndi namwali, makanda, ndi akazi; koma musayandikira munthu aliyense ali nacho chizindikiro, ndipo muyambe pa malo anga opatulika. Pamenepo anayamba ndi akuluwo anali pakhomo pa nyumba. Nati kwa iwo, Muipse nyumbayi ndi kudzaza mabwalo ndi ophedwa, mukani. Ndipo anatuluka, nakantha m'mudzimo. Ndipo kunali, alimkukantha iwo, nditatsala ine, ndinagwa nkhope yanga pansi, ndi kufuula, ndi kuti, Kalanga ine, Ambuye Mulungu! Kodi mudzaononga otsala onse a Israele pakutsanulira ukali wanu pa Yerusalemu? Pamenepo ananena nane, Mphulupulu ya nyumba ya Israele ndi Yuda ndi yaikulukulu ndithu, ndi dziko ladzala ndi mwazi, ndi mudziwo wadzala ndi kukhotetsa milandu; pakuti ati, Yehova wataya dziko, Yehova sapenya. Ndipo Inenso diso langa silidzalekerera, wosachita chifundo Ine, koma ndidzawabwezera njira yao pamtu pao. Ndipo taonani, munthu wovala bafutayo, wokhala ndi zolembera nazo m'chuuno mwake, anabweza mau, ndi kuti, Ndachita monga munandilamulira ine. Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, kuthambo lokhala pamwamba pa mitu ya akerubi kudaoneka ngati mwala wasafiro, ngati maonekedwe a chifaniziro cha mpando wachifumu pamwamba pao. Ndipo Yehova analankhula ndi munthu wovala bafuta, nati, Lowa pakati pa njingazi pansi pa kerubi, nudzaze manja ako makala a moto ochokera pakati pa akerubi, nuwamwaze pamwamba pa mudzi. Nalowa, ndili chipenyere ine. Tsono akerubi anaima kudzanja lamanja la nyumba polowa munthuyo, ndi mtambo unadzaza bwalo la m'kati. Ndipo ulemerero wa Yehova unakwera kuchokera kukerubi kunka kuchiundo cha nyumba; ndi nyumba inadzala nao mtambo, ndi bwalo linadzala ndi cheza cha ulemerero wa Yehova. Ndipo mkokomo wa mapiko a akerubi unamveka mpaka bwalo lakunja, ngati mau a Mulungu Wamphamvuyonse, pakunena Iye. Ndipo kunali pomlamulira munthu wovala bafutayo, ndi kuti, Para moto pakati pa njingazi ndi pakati pa akerubi; iye analowa, naima m'mbali mwa njinga. Pamenepo kerubi wina anatambasula dzanja lake pakati pa akerubi kumoto uli pakati pa akerubi, napalako, nauika m'manja mwa iye wovala bafuta, ndiye naulandira, natuluka. Ndipo panaoneka pa akerubi chonga dzanja la munthu pansi pa mapiko ao. Pamenepo ndinapenya, ndipo taonani, njinga zinai m'mbali mwa akerubi, njinga imodzi m'mbali mwa kerubi mmodzi, ndi njinga ina m'mbali mwa kerubi wina, ndi maonekedwe a njingazi ananga mawalidwe a berulo. Ndipo maonekedwe ake, zonse zinai zinafanana, ngati njinga ziwiri zopingasitsana. Pakuyenda akerubi anayenda kumbali zao zinai, sanatembenuke poyenda; koma komwe udalozako mutu anatsatako, sanatembenuke poyenda. Ndipo thupi lao lonse, ndi misana yao, ndi manja ao, ndi mapiko ao, ndi njinga zomwe, zinadzala ndi maso pozungulira pao, zingakhale njingazi anai aja anali nazo. Kunena za njingazi, wina anazifuulira, ndili chimvere ine, Kunkhulirani. Ndipo aliyense anali nazo nkhope zinai, nkhope yoyamba ndiyo nkhope ya kerubi, ndi nkhope yachiwiri ndiyo nkhope ya munthu, ndi yachitatu ndiyo nkhope ya mkango, ndi yachinai ndiyo nkhope ya chiombankhanga. Pamenepo akerubi anakwera, ndizo zamoyo zija ndinaziona kumtsinje Kebara. Ndipo pakuyenda akerubi, njinga zinayenda pambali pao, ndi pakutambasula mapiko ao akerubiwo kuuluka padziko, njingazi sizinatembenuka pambali pao. Pakuima iwo zinaima izi, ndi pakukwera iwo izi zinakwera pamodzi nao; pakuti mzimu wa zamoyozo unali mwa izo. Ndipo ulemerero wa Yehova unachoka pa chiundo cha nyumba, nuima pamwamba pa akerubi. Ndipo akerubi anatambasula mapiko ao, nauluka padziko, ndili chipenyere, pakuchoka iwo ndi njingazi pa mbali pao; ndipo anaima pa chitseko cha chipata cha kum'mawa cha nyumba ya Yehova, ndi ulemerero wa Mulungu wa Israele unali pamwamba pao. Awa ndi zamoyozo ndinaziona pansi pa Mulungu wa Israele kumtsinje Kebara, ndipo ndinadziwa kuti ndiwo akerubi. Yense anali nazo nkhope zinai, ndi yense mapiko anai, ndi chifaniziro cha manja a munthu pansi pa mapiko ao. Ndi chifaniziro cha nkhope zao ndicho nkhope zomwezo ndinaziona kumtsinje Kebara, maonekedwe ao ndi iwo eni; aliyense anayenda, nalunjika m'tsogolo. Pamenepo unandikweza mzimu, nudza nane kuchipata cha kum'mawa cha nyumba ya Yehova choloza kum'mawa; ndipo taonani, pa chitseko cha chipata amuna makumi awiri mphambu asanu; ndipo ndinaona pakati pao Yazaniya mwana wa Azuri ndi Pelatiya mwana wa Benaya, akalonga a anthu. Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, awa ndi anthu olingirira za mphulupulu, ndi kupangira uphungu woipa m'mudzi muno; ndiwo akuti, siinafike nyengo yakumanga nyumba; mudzi uwu ndi mphika, ife ndife nyama. Chifukwa chake uwanenere, neneratu, wobadwa ndi munthu iwe. Pamenepo mzimu wa Yehova unandigwera, ndipo anati kwa ine, Nena, Atero Yehova, Mwatero nyumba ya Israele, pakuti ndidziwa zimene zimalowa m'mtima mwanu. Mwachulukitsa ophedwa anu m'mudzi muno, mwadzazanso makwalala ake ndi ophedwawo. Chifukwa chake atero Yehova Mulungu, Ophedwa anu munawaika m'kati mwake, iwo ndiwo nyama imene, ndi mudzi uwu ndiwo mphika; koma inu mudzatulutsidwa m'kati mwake. Mwaopa lupanga, tsono ndidzakufikitsirani lupanga, ati Yehova Mulungu. Ndipo ndidzakutulutsani m'kati mwake, ndi kukuperekani m'manja a alendo, ndi kuchita maweruzo pakati panu. Mudzagwa ndi lupanga, ndidzakuweruzirani kumalire a Israele; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Mudzi uno sudzakhala mphika wanu, ndi inu simudzakhala nyama m'kati mwake, ndidzakuweruzirani kumalire a Israele; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuti simunayenda m'malemba anga, kapena kuchita maweruzo anga, koma mwachita monga mwa maweruzo a amitundu okhala pozungulira panu. Ndipo kunali, pakunenera ine, anamwalira Pelatiya mwana wa Benaya. Pamenepo ndinagwa nkhope yanga pansi, ndi kufuula ndi mau akulu, ndi kuti, Kalanga ine, Yehova Mulungu? Mudzatsiriza kodi otsala a Israele? Ndipo mau a Yehova anandidzera kuti, Wobadwa ndi munthu iwe, abale ako, inde abale ako amuna a chibale chako, ndi nyumba yonse ya Israele, yonseyi ndiwo amene okhala m'Yerusalemu ananena nao, Muzikhala kutali kwa Yehova; dziko ili lapatsidwa kwa ife, likhale cholowa chathu; chifukwa chake uziti, Atero Yehova Mulungu, Ngakhale ndawachotsa kutali mwa amitundu, ngakhalenso ndawabalalikitsa m'maiko, koma ndidzawakhalira malo opatulika kanthawi kumaiko adafikako. Chifukwa chake uziti, Atero Yehova Mulungu, Ndidzakumemezani kumitundu ya anthu, ndi kukusonkhanitsani muchoke m'maiko m'mene munabalalikiramo, ndipo ndidzakuninkhani dziko la Israele. Ndipo adzafikako, nadzachotsako zonyansa zake zonse, ndi zake zonse zakuipitsamo. Ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi, ndi kuika mzimu watsopano m'kati mwao; ndipo ndidzawachotsera mtima wamwala m'thupi mwao, ndi kuwapatsa mtima wamnofu; kuti ayende m'malemba anga, ndi kusunga maweruzo anga, ndi kuwachita; ndipo adzakhala anthu anga, ndi Ine ndidzakhala Mulungu wao. Koma iwo amene mtima wao unatsata mtima wa zonyansa zao, ndi zoipitsitsa zao, ndidzawabwezera njira yao pamtu pao, ati Yehova Mulungu. Pamenepo akerubi anatambasula mapiko ao, ndi njinga zinali pa mbali pao; ndi ulemerero wa Mulungu wa Israele unali pamwamba pao. Ndipo ulemerero wa Yehova unakwera kuchoka pakati pa mudzi, nuima pa phiri la kum'mawa kwa mudzi. Ndipo mzimu unandikweza, nufika nane m'masomphenya mwa mzimu wa Mulungu kudziko la Ababiloni, kwa andendewo. M'mwemo masomphenya ndidawaona anandichokera, nakwera. Pamenepo ndinanena ndi andendewo zonse zija adandionetsa Yehova. Mau a Yehova anandidzeranso, ndi kuti, Wobadwa ndi munthu iwe, ukhala pakati pa nyumba yampanduko, yokhala nao maso akuonera, koma osaona; ndi makutu akumvera, koma osamva; pakuti iwo ndiwo nyumba yampanduko. Potero wobadwa ndi munthu iwe, udzikonzeretu akatundu a pa ulendo wa kundende, nuchoke usana pamaso pao, uchoke pokhala iwepo kunka malo ena pamaso pao; kapena adzachizindikira, angakhale ndiwo nyumba yopanduka. Uzitulutsa akatundu ako usana pamaso pao, ngati a pa ulendo wa kundende; ndipo madzulo uzituluka wekha pamaso pao, monga amatuluka olowa kundende. Udziboolere khoma pamaso pao, nuwatulutsire akatundu pamenepo. Pamaso pao uwasenze paphewa pako, ndi kuwatulutsa kuli mdima, nuphimbe nkhope yako kuti usapenye dziko; popeza ndakuika chizindikiro cha nyumba ya Israele. Ndipo ndinachita monga momwe anandilamulira, ndinatulutsa akatundu anga usana, ngati a pa ulendo wa kundende, ndi madzulo ndinaboola pakhoma ndi dzanja langa, ndinawatulutsa pali mdima, ndi kuwasenza paphewa panga pamaso pao. Ndipo m'mawa mau a Yehova anandidzera, ndi kuti, Wobadwa ndi munthu iwe, kodi nyumba ya Israele, nyumba yampanduko, siinati kwa iwe, Uchitanji? Unene nao, Atero Ambuye Yehova, Katundu uyu anena za kalonga wa m'Yerusalemu, ndi nyumba yonse ya Israele yokhala pakati pao. Uziti, Ine ndine chizindikiro chanu, monga ndachita ine momwemo kudzachitidwa nao; adzachotsedwa kunka kundende. Kalongayo ali pakati pao adzasenza paphewa pake mumdima, nadzatuluka; adzaboola palinga, nadzatulutsapo; adzaphimba nkhope yake kuti asapenye dziko ndi maso ake. Ndidzamphimba ndi ukonde wanga, nadzakodwa iye mu msampha wanga; ndipo ndidzafika naye ku Babiloni, ku dziko la Ababiloni; sadzaliona, chinkana adzafako. Ndipo onse omzinga kumthandiza, ndi magulu ake onse, ndidzawamwaza kumphepo zonse, ndidzawasololeranso lupanga lakuwatsata. Motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuwamwaza Ine mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa m'maiko. Koma ndidzawasiya owerengeka apulumuke lupanga, ndi njala, ndi mliri, kuti afotokoze zonyansa zao kwa amitundu kumene afikako; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Anandidzeranso mau a Yehova, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, udye mkate wako ndi kunthunthumira, ndi kumwa madzi ako ndi kunjenjemera, ndi kutenga nkhawa; nunene kwa anthu a m'dziko, Atero Yehova Mulungu za iwo okhala m'Yerusalemu, ndi za dziko la Israele, Adzadya mkate wao ndi nkhawa, ndi kumwa madzi ao ndi kusumwa; pakuti dziko lao lidzakhala lachipululu, kuleka kudzala kwake chifukwa cha chiwawa cha onse okhalamo. Ndi midzi yokhalamo anthu idzapasuka, ndi dziko lidzakhala labwinja; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, ngwotani mwambi umene muli nao m'dziko la Israele, wakuti, Masiku achuluka, ndi masomphenya ali onse apita pachabe? Chifukwa chake unene nao, Atero Yehova Mulungu, Ndidzaleketsa mwambi uwu, ndipo sadzautchulanso mwambi m'Israele; koma unene nao, Masiku ayandikira, nadzachitika masomphenya ali onse. Pakuti sikudzakhalanso masomphenya achabe, kapena ula wosyasyalika m'nyumba ya Israele. Pakuti Ine ndine Yehova, ndidzanena, ndi mau ndidzanenawo adzachitika, osazengerezekanso; pakuti m'masiku anu, nyumba yopanduka inu, ndidzanena mau ndi kuwachita, ati Yehova Mulungu. Anandidzeranso mau a Yehova, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, taona, iwo a nyumba ya Israele akuti, masomphenya awaona ndiwo a masiku ambiri; ndipo anenera za nthawi zili kutali. Chifukwa chake uziti nao, Atero Ambuye Yehova, Palibe amodzi a mau anga adzazengerezekanso; koma mau ndidzanenawo adzachitika, ati Ambuye Yehova. Ndipo mau a Yehova anandidzera ine, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, Unenere za aneneri a Israele onenerawo, nuziti nao onenera za m'mtima mwaomwao, Tamverani mau a Yehova. Atero Ambuye Yehova, Tsoka aneneri opusawo akutsata mzimu waowao, chinkana sanaone kanthu. Aneneri ako, Israele, akhala ngati nkhandwe m'mapululu. Simunakwera kuima mopasuka, kapena kumanganso linga la nyumba ya Israele, kuima kunkhondo tsiku la Yehova. Iwo aona zopanda pake, ndi phenda labodza amene anena, Atero Yehova; koma Yehova sanawatume, nayembekezetsa anthu kuti mauwo adzakhazikika. Simunaona masomphenya opanda pake kodi? Simunanena ula wabodza kodi? Pakunena inu, Atero Yehova; chinkana sindinanena? Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza mwanena zopanda pake, ndi kuona mabodza, chifukwa chake taonani, ndikhala Ine wotsutsana nanu, ati Ambuye Yehova. Ndi dzanja langa lidzakhala lotsutsana nao aneneri akuona zopanda pake, ndi kupenda za bodza; sadzakhala mu msonkhano wa anthu anga, kapena kulembedwa m'buku lolembedwamo nyumba ya Israele; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova. Popeza, inde popeza asokeretsa anthu anga, ndi kuti, Mtendere, pokhala palibe mtendere; ndipo anthu akamanga linga, aneneriwo alimata ndi dothi losapondeka; uziti nao olimata ndi dothi losapondeka, kuti lidzagwa, lidzavumbidwa ndi mvula yaikulu; ndi inu, matalala akulu, mudzagwa; ndi mkuntho udzalithithimula. Ndipo taonani, litagwa linga, sadzanena nanu kodi, Lili kuti dothi munalimata nalo? Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Ndidzalithithimula ndi mkuntho m'ukali wanga; ndipo lidzavumbidwa ndi mvula yaikulu mu mkwiyo wanga, ndi matalala akulu adzalitha m'ukali wanga. M'mwemo ndidzagumula linga munalimata ndi dothi losapondeka, ndi kuligwetsa pansi; kuti maziko ake agadabuke, ndipo lidzagwa; ndi inu mudzathedwa pakati pake; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. M'mwemo ndidzakwaniritsa ukali wanga pa lingalo, ndi pa iwo analimata ndi dothi losapondeka, ndipo ndidzati kwa inu, Lingalo palibe, ndi olimata palibe, ndiwo aneneri a Israele akunenera za Yerusalemu, nauonera masomphenya a mtendere, pamene palibe mtendere, ati Ambuye Yehova. Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, uziika nkhope yako itsutsane nao ana akazi a anthu ako, akunenera za m'mtima mwao, nunenere chowatsutsa, nuziti, Atero Ambuye Yehova, Tsoka akazi osoka zophimbira mfundo zonse za dzanja, ndi iwo okonza zokuta mitu za misinkhu iliyonse, kuti asake miyoyo! Kodi musaka miyoyo ya anthu anga ndi kudzisungira miyoyo yanu? Ndipo mundidetsa mwa anthu anga kulandirapo barele wodzala manja, ndi zidutsu za mkate, kuipha miyoyo yosayenera kufa, ndi kusunga miyoyo yosayenera kukhala ndi moyo, ndi kunena mabodza kwa anthu anga omvera bodza. Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taonani, nditsutsana nazo zophimbira zanu, zimene musaka nazo miyoyo komweko, kuiuluza; ndipo ndidzazikwatula m'manja mwanu, ndi kuimasula, ndiyo miyoyo muisaka kuiuluza. Zokuta mitu zanu zomwe ndidzazing'amba, ndi kulanditsa anthu anga m'manja mwanu; ndipo sadzakhalanso m'mphamvu mwanu kusakidwa; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Popeza mwamvetsa chisoni ndi mabodza mtima wa wolungama, amene sindinamvetsa chisoni Ine, ndi kumlimbitsa manja woipa, kuti asabwerere kuleka njira yake yoipa, ndi kusungidwa wamoyo; chifukwa chake simudzaonanso zopanda pake, kapena kupenda; koma ndidzalanditsa anthu anga m'manja mwanu; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Pamenepo anafika kwa ine akulu ena a Israele nakhala pansi pamaso panga. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, anthu awa anautsa mafano ao mumtima mwao, naimika chokhumudwitsa cha mphulupulu yao pamaso pao; ndifunsidwe nao konse kodi? Chifukwa chake ulankhule nao, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Aliyense wa nyumba ya Israele wakuutsa mafano ake mumtima mwake, naimika chokhumudwitsa cha mphulupulu yake pamaso pake, nadza kwa mneneri, Ine Yehova ndidzamyankhapo monga mwa mafano ake aunyinji; kuti ndigwire nyumba ya Israele mumtima mwao; popeza onsewo asanduka alendo ndi Ine mwa mafano ao. Chifukwa chake uziti kwa nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Bwerani, lekani mafano anu, tembenuzani nkhope zanu kuzisiya zonyansa zanu zonse. Pakuti aliyense wa nyumba ya Israele, kapena wa alendo ogonera m'Israele, wodzisiyanitsa kusatsata Ine, nautsa mafano ake m'mtima mwake, naimika chokhumudwitsa cha mphulupulu yake pamaso pake, nadzera mneneri kudzifunsira kwa Ine, Ine Yehova ndidzamyankha ndekha; ndipo ndidzaikira munthu uyu nkhope yanga imtsutse, ndi kumuyesa chodabwitsa, ndi chizindikiro, ndi mwambi, ndi kumsadza pakati pa anthu anga; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Ndipo akacheteka mneneriyo, nakanena mau, Ine Yehova ndamcheta mneneri uja; ndipo ndidzamtambasulira dzanja langa, ndi kumuononga pakati pa anthu anga Israele. Ndipo adzasenza mphulupulu yao, mphulupulu ya mneneri idzanga mphulupulu ya uja wamfunsira; kuti nyumba ya Israele isasocherenso kusatsata Ine, kapena kudzidetsanso ndi zolakwa zao zonse; koma kuti akhale anthu anga, ndipo ndikhale Ine Mulungu wao, ati Ambuye Yehova. Ndipo anandidzera mau a Yehova akuti, Likandichimwira dziko ndi kuchita monyenga, ndipo ndikalitambasulira dzanja langa, ndi kulithyolera mchirikizo wake, ndiwo mkate, ndi kulitumizira njala, ndi kulidulira munthu ndi nyama, chinkana akadakhala m'mwemo anthu awa atatu, Nowa, Daniele, ndi Yobu, akadapulumutsa moyo wao wokha mwa chilungamo chao, ati Ambuye Yehova. Ndikapititsa zilombo zoipa pakati pa dziko, nizipulula ana, kuti likhale lachipululu losapitako munthu chifukwa cha zilombo, chinkana anthu omwewo atatu akadakhala m'mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sakadapulumutsa ana amuna kapena akazi; iwo akadapulumuka okha; koma dziko likadakhala lachipululu. Kapena ndikadza pa dziko ndi lupanga, ndi kuti, Lupanga lipite pakati pa dziko, kuti ndilidulire munthu ndi nyama; chinkana anthu atatuwo akadakhala m'mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sakadapulumutsa ana amuna kapena akazi; koma iwo akadapulumuka okha. Kapena ndikatumizira dzikolo mliri, ndi kulitsanulira ukali wanga ndi mwazi, kulidulira munthu ndi nyama; chinkana Nowa, Daniele, ndi Yobu, akadakhala m'mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sakadapulumutsa ana amuna kapena akazi; akadapulumutsa moyo wao wokha ndi chilungamo chao. Pakuti atero Ambuye Yehova, Kopambana kotani nanga ndikatumizira Yerusalemu maweruzo anga anai owawa, lupanga, njala, zilombo zoipa, ndi mliri, kuudulira anthu ndi nyama? Koma onani mudzatsala opulumuka m'mwemo amene adzatulutsidwa, ndiwo ana aamuna ndi aakazi; taonani, adzatuluka kudza kwa inu; ndipo mudzaona njira zao, ndi zochita zao; mudzatonthozedwanso pa zoipa ndazitengera pa Yerusalemu, inde pa zonse ndazitengerapo. Ndipo adzakusangalatsani pamene muona njira yao, ndi zochita zao; ndipo mudzadziwa kuti sindinazichita kopanda chifukwa zonse ndinazichita momwemo, ati Ambuye Yehova. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, mtengo wampesa uposeranji mtengo uliwonse wina, nthambi ya mpesa yokhalayo mwa mitengo ya kunkhalango? Kodi atengako mtengo kupanga nao ntchito? Atengako chichiri kodi kupachikapo chipangizo chilichonse? Taona, auponya kumoto kuuyesa nkhuni, moto unyeketsa nsonga zake zonse ziwiri, nupserera pakati pake, kodi ukomera ntchito iliyonse? Taonani, pokhala wamphumphu sunayenera ntchito iliyonse, nanga utanyeketsa moto nupserera udzayeneranso ntchito iliyonse? Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Ngati mtengo wampesa pakati pa mitengo ya kunkhalango ndauponya kumoto ukhale nkhuni, momwemo ndidzapereka okhala m'Yerusalemu. Ndipo ndidzaika nkhope yanga iwatsutse; adzatuluka kumoto, mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuika Ine nkhope yanga iwatsutse. Ndipo ndidzasandutsa dziko chipululu; popeza anachita cholakwa, ati Ambuye Yehova. Anandidzeranso mau a Yehova, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, Dziwitsa Yerusalemu zonyansa zake, nuziti, Atero Ambuye Yehova kwa Yerusalemu, Chiyambi chako ndi kubadwa kwako ndiko kudziko la Akanani; atate wako anali Mwamori, ndi mai wako Muhiti. Ndipo za kubadwa kwako, tsiku lobadwa iwe sanadule nchofu yako, sanakuyeretse ndi kukusambitsa ndi madzi, sanakuthire mchere konse, kapena kukukulunga m'nsalu ai. Panalibe diso linakuchitira chifundo, kukuchitira chimodzi chonse cha izi, kuchitira iwe nsoni; koma unatayidwa kuyere; pakuti ananyansidwa nao moyo wako tsiku la kubadwa kwako. Ndipo popita Ine panali iwepo, ndinakuona ulikuvimvinizika m'mwazi mwako. Pamenepo ndinanena ndi iwe m'mwazi wako. Khala ndi moyo, inde ndinati kwa iwe m'mwazi mwako, Khala ndi moyo. Ndinakuchulukitsa ngati mphundu za kumunda; ndipo unathululuka ndi kukula kufikira wakongola nkhope, mawere ako anamera, ndi tsitsi lako linamera; koma unali wamaliseche ndi wausiwa. Ndipo popita Ine panali iwepo ndi kukupenya, taona nyengo yako ndiyo nyengo yakukondana; pamenepo ndinakufunda chofunda changa, ndi kuphimba umaliseche wako; inde ndinakulumbirira ndi kupangana nawe, ati Ambuye Yehova, ndipo unakhala wanga. Ndipo ndinakusambitsa ndi madzi, inde ndinakutsuka kukuchotsera mwazi wako, ndi kukudzoza mafuta. Ndinakuvekanso ndi nsalu zopikapika, ndi kukuveka nsapato za chikopa cha katumbu; ndinakuzenenga nsalu yabafuta, ndi kukuphimba ndi nsalu yasilika. Ndinakukometseranso ndi zokometsera, ndi kuika zigwinjiri m'manja mwako, ndi unyolo m'khosi mwako. Momwemo ndinaika chipini m'mphuno mwako, ndi maperere m'makutu mwako, ndi korona wokongola pamutu pako. Ndipo unadzikometsera ndi golide, ndi siliva, ndi chovala chako ndi bafuta ndi silika ndi yopikapika; unadya ufa wosalala, ndi uchi, ndi mafuta; ndipo unali wokongola woposa ndithu, ndipo unapindulapindula kufikira unasanduka ufumu. Ndi mbiri yako inabuka mwa amitundu chifukwa cha kukongola kwako; pakuti ndiko kwangwiro, mwa ulemerero wanga ndinauika pa iwe, ati Ambuye Yehova. Koma unatama kukongola kwako, ndi kuchita zachigololo potama mbiri yako, ndi kutsanulira zigololo zako pa munthu aliyense wopitapo; unali wake. Ndipo unatengako zovala zako, ndi kudzimangira misanje ya mawangamawanga, ndi kuchitapo chigololo; zotere sizinayenera kufika kapena kuchitika. Unatenganso zokometsera zako zokoma za golide wanga ndi siliva wanga, zimene ndinakupatsa, ndi kudzipangira mafano a amuna, ndi kuchita nao chigololo. Unatenganso zovala zako za nsalu yopikapika, ndi kuwaveka nazo, unaikanso mafuta anga ndi chofukiza changa pamaso pao. Ndi mkate wanga ndinakupatsawo, ufa wosalala, ndi mafuta, ndi uchi, ndinakudyetsazo, unawaikira izi pamaso pao, zichite fungo lokoma; kunatero, ati Ambuye Yehova. Unatenganso ana ako aamuna ndi aakazi amene unandibalirawo, ndi kuwapereka nsembe awathe. Zigololo zako zidachepa kodi, kuti unawapha ana anga ndi kuwapereka, pakuwapititsa pamoto? Ndipo pa zonyansa zako zonse ndi zigololo zako sunakumbukira masiku a ubwana wako, muja unakhala wamaliseche ndi wausiwa, wovimvinizika m'mwazi wako. Ndipo kudachitika utatha zoipa zako zonse, (tsoka iwe, tsoka, ati Ambuye Yehova) unadzimangira nyumba yachimphuli, unadzimangiranso chiunda m'makwalala ali onse. Unamanga chiunda chako pa mphambano zilizonse, ndipo unanyansitsa kukongola kwako, ndi kutukula mapazi ako kwa yense wopitako, ndi kuchulukitsa chigololo chako. Wachitanso chigololo ndi Ejipito oyandikizana nawe, akulu thupi, ndi kuchulukitsa chigololo chako kuutsa mkwiyo wanga. Taona tsono, ndakutambasulira dzanja langa, ndi kuchepsa gawo lako la chakudya, ndi kukupereka ku chifuniro cha iwo akudana nawe, kwa ana akazi a Afilisti akuchita manyazi ndi njira yako yoipa. Unachitanso chigololo ndi Aasiriya, pakuti unakhala wosakoledwa, inde unachita chigololo nao, koma sunakoledwa. Unachulukitsanso chigololo chako m'dziko la Kanani, mpaka dziko la Ababiloni, koma sunakoledwa nachonso. Ha? Mtima wako ngwofooka, ati Ambuye Yehova, pakuchita iwe izi zonse, ndizo ntchito za mkazi wachigololo wouma m'maso. Pakumanga nyumba yako yachimphuli pa mphambano zilizonse, ndi pomanga chiunda chako m'makwalala ali onse, sunakhala ngati mkazi wadama waphindu, popeza unapeputsa mphotho. Ndiwe mkazi wokwatibwa wochita chigololo, wolandira alendo m'malo mwa mwamuna wake. Anthu amaninkha akazi onse achigololo mphatso, koma iwe umaninkha mabwenzi ako onse mphatso zako ndi kuwalipira, kuti akudzere kuchokera kumbali zonse, kuti achite nawe chigololo. M'mwemo usiyana konse ndi akazi ena m'chigololo chako; pakuti palibe wokutsata kuchita nawe chigololo; popezanso uwalipira, koma sakupatsa iwe mphotho; potero usiyana nao konse ena. Chifukwa chake, wachigololo iwe, tamvera mau a Yehova: Atero Ambuye Yehova, Popeza ndalama zako zamwazika, nuvundukuka umaliseche wako mwa chigololo chako ndi mabwenzi ako, ndi chifukwa cha mafano onse a zonyansa zako, ndi mwazi wa ana ako umene unawapatsa; chifukwa chake taona, ndidzasonkhanitsa mabwenzi ako onse amene wakondwera nao, ndi onse unawakonda, pamodzi ndi onse unawada; inde ndidzawasonkhanitsira iwe pozungulira ponse, ndi kuwavundukulira umaliseche wako, kuti aone umaliseche wako wonse. Ndipo ndidzaweruza mlandu wako, monga aweruza akazi achigololo ndi okhetsa mwazi; ndipo ndidzakutengera mwazi wa ukali ndi wa nsanje. Ndidzakuperekanso m'dzanja lao, ndipo adzagwetsa nyumba yako yachimphuli, ndi kugumula ziunda zako, nadzakuvula zovala zako, ndi kulanda zokometsera zako zokongola, nadzakusiya wamaliseche ndi wausiwa. Ndipo adzamemezera iwe msonkhano, nadzakuponya miyala, ndi kukupyoza ndi malupanga ao. Ndipo adzatentha nyumba zako ndi moto, nadzakuweruza pamaso pa akazi ambiri; ndipo ndidzakuleketsa kuchita chigololo, ndipo sudzalipiranso mphotho yachigololo. M'mwemo ukali wanga udzakhuta nawe, ndi nsanje yanga idzakuchokera, ndipo ndidzakhala chete wosakwiyanso. Popeza sunakumbukira masiku a ubwana wako, koma wandivuta nazo zonsezi, chifukwa chake taona, Inenso ndidzakubwezera njira yako pamutu pako, ati Ambuye Yehova; ndipo sudzachita choipa ichi choonjezerapo pa zonyansa zako zonse. Taona, aliyense wonena miyambi adzakunenera mwambi uwu, wakuti, Monga make momwemo mwana wake. Iwe ndiwe mwana wa mai ako wonyansidwa naye mwamuna wake ndi ana ake, ndipo iwe ndiwe mng'ono wao wa akulu ako akunyansidwa ndi amuna ao ndi ana ao; mai wako ndiye Muhiti, ndi atate wako ndiye Mwamori. Ndi mkulu wako ndiye Samariya, wokhala kudzanja lako lamanzere, iye ndi ana ake akazi; ndi mng'ono wako wokhala kudzanja lako lamanja ndiye Sodomu ndi ana ake akazi. Koma sunayenda m'njira zao, kapena kuchita monga mwa zonyansa zao pang'ono pokha; unawaposa iwo m'kuvunda kwako, m'njira zako zonse. Pali Ine, ati Ambuye Yehova, Sodomu mng'ono wako sanachita, iye kapena ana ake akazi, monga umo unachitira iwe ndi ana ako akazi. Taona, mphulupulu ya mng'ono wako Sodomu ndi iye, kudzikuza, kuchuluka kwa chakudya, ndi kupumula kwa mtambasali, anali nako iye ndi ana ake; ndipo sanalimbitse dzanja la wosauka ndi wosowa. Ndipo anadzikuza, nachita chonyansa pamaso panga; chifukwa chake ndinawachotsa pakuchiona. Ngakhale Samariya sanachite theka la zochimwa zako, koma unachulukitsa zonyansa zako, kuwaposa iwowa, ndi kuika abale ako olungama ndi zonyansa zako zonse unazichita. Usenzenso manyazi ako, iwe wakuweruza abale ako mwa zochimwa zako unazichita monyansa koposa iwowa; iwo akuposa iwe m'chilungamo chao, nawenso uchite manyazi nusenze manyazi ako, popeza waika abale ako olungama. Ndipo ndidzabweza undende wao, undende wa Sodomu ndi ana ake, ndi undende wa Samariya ndi ana ake, ndi undende wa andende ako pakati pao; kuti usenze manyazi ako, ndi kuti uchite manyazi chifukwa cha zonse unazichita pakuwatonthoza. Ndipo abale ako Sodomu ndi ana ake adzabwerera umo unakhalira kale, ndipo Samariya ndi ana ake adzabwerera umo anakhalira kale; ndi iwe ndi ana ako mudzabwerera umo munakhalira kale. Ndipo sunakamba za mbale wako Sodomu pakamwa pako tsiku la kudzikuza kwako; chisanavundukuke choipa chako monga nthawi ya chitonzo cha ana akazi a Aramu, ndi onse akumzungulira iye, ana akazi a Afilisti akupeputsa pozungulira ponse. Wasenza choipa chako ndi zonyansa zako, ati Yehova. Pakuti atero Ambuye Yehova, Ndidzachita ndi iwe monga umo unachitira; popeza wapepula lumbiro ndi kuthyola pangano. Koma ndidzakumbukira Ine pangano langa ndi iwe m'masiku a ubwana wako, ndipo ndidzakhazikitsa pangano losatha nawe. Pamenepo udzakumbukira njira zako ndi kuchita manyazi, pakulandira abale ako akulu ndi ang'ono; ndipo ndidzakupatsa awa akhale ana ako akazi, angakhale sali a pangano lako. Pakuti ndidzakhazikitsa pangano langa ndi iwe, ndipo udzadziwa kuti Ine ndine Yehova; kuti uzikumbukira ndi kuchita manyazi ndi kusatsegulanso pakamwa pako konse, chifukwa chamanyazi ako, pamene ndikufafanizira zonse unazichita, ati Ambuye Yehova. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, ipha mwambi, nunene fanizo kwa nyumba ya Israele, nuziti, Atero Ambuye Yehova, Chiombankhanga chachikulu ndi mapiko akulu, ndi maphiphi atali, odzala nthenga cha mathothomathotho, chinafika ku Lebanoni, nichitenga nsonga ya mkungudza, chinabudula nsonga yosomphoka ya nthambi zake zanthete, ndi kumuka nayo kudziko la malonda, chinaiika m'mudzi wa amalonda. Chinatengakonso mbeu ya m'dziko, ndi kuibzala m'nthaka yokoma, chinaiika panali madzi ambiri, chinaioka ngati mtengo wamsondodzi. Ndipo inaphuka, nikhala mpesa wotambalala waufupi msinkhu, nthambi zake zinapindikira momwe, ndi mizu yake pansi pake, nikhala mpesa, nuonetsa nthambi ndi kuphuka mphukira. Panalinso chiombankhanga china chachikulu, ndi mapiko akulu, ndi nthenga zambiri; ndipo taona, mpesa uwu unachipindira mizu yake, nuchilunjikitsira nthambi zake, kuchokera pookedwa pake, kuti chiuthirire madzi. Unaokedwa mu nthaka yabwino kuli madzi ambiri, kuti uphuke nthambi, nubale zipatso, nukhale mpesa wabwino. Uziti, Atero Ambuye Yehova, Udzakondwa kodi? Sadzausula ndi kudula zipatso zake, kuti uume, kuti masamba ake onse ophuka aume, ngakhale palibe mphamvu yaikulu, kapena anthu ambiri akuuzula? Inde ungakhale waokedwa udzakondwa kodi? Sudzauma chiumire kodi pakuuomba mphepo ya kum'mawa? Udzauma pookedwa apo udaphuka. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti. Uziti, tsono kwa nyumba ya mpandukoyi, Simudziwa kodi izi nchiyani? Uziti, Taonani mfumu ya ku Babiloni inadza ku Yerusalemu, nitenga mfumu yake ndi akalonga ake, nibwera nao kuli iye ku Babiloni; nitenga wa mbumba yachifumu, nichita naye pangano, nimlumbiritsa, nichotsa amphamvu a m'dziko; kuti ufumuwo ukhale wopepuka, kuti usadzikweze, koma kuti pakusunga pangano lake ukhale. Koma anapandukira ndi kutuma mithenga yake ku Ejipito, kuti ampatse akavalo ndi anthu ambiri. Adzapindula kodi? Adzapulumuka wakuchita izi? Athyole pangano ndi kupulumuka kodi? Pali Ine, ati Ambuye Yehova, pamalo pokhala mfumu, imene idamchititsa ufumu, imene anapeputsa lumbiro lake, imene anathyola pangano lake, adzafa pamodzi ndi iye pakati pa Babiloni. Ndipo Farao ndi nkhondo yake yaikulu, ndi khamu lake launyinji, sadzachita pamodzi naye kunkhondo, pakuunda mtumbira, ndi kumanga malinga, kulikha anthu ambiri. Pakuti anapepula lumbiro, ndi kuthyola pangano, angakhale anapereka dzanja lake; popeza anachita izi zonse sadzapulumuka. Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Pali Ine, lumbiro langa, analipepula, ndi pangano langa analithyola, ndidzawabweza pamutu pake. Ndidzamphimbanso ndi ukonde wanga, nadzakodwa iye mu msampha wanga; ndipo ndidzadza naye ku Babiloni, ndi kunena naye komweko mlandu wa kulakwa kwake anandilakwira nako. Ndipo othawa ake onse m'magulu ake onse adzagwa ndi lupanga, ndi otsala adzabalalitsidwa kumphepo zonse; ndipo mudzadziwa kuti Ine Yehova ndanena. Atero Ambuye Yehova, Ndidzatenganso nsonga ya mkungudza wautali ndi kuiika; ndidzabudula nsonga yosomphoka ya nthambi zake zanthete, ndi kuioka pa phiri lalitali lothuvuka; pa phiri lothuvuka la Israele ndidzaioka, ndipo idzaphuka nthambi ndi kubala zipatso, nidzakhala mkungudza wokoma, ndi m'munsi mwake mudzakhala mbalame zilizonse za mapiko ali onse; mu mthunzi wa nthambi zake zidzabindikira. Ndipo mitengo yonse ya kuthengo idzadziwa kuti Ine Yehova ndatsitsa mtengo wosomphoka, ndakuza mtengo waung'ono, ndaumitsa mtengo wauwisi, ndi kuphukitsa mtengo wouma; Ine Yehova ndanena ndi kuchichita. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti, Mutani inu ndi kunena mwambi uwu za dziko la Israele, wakuti, Atate adadya mphesa zosacha, ndi mano a ana ayayamira. Pali Ine, ati Ambuye Yehova, simudzaonanso chifukwa cha kunena mwambiwu m'Israele. Taonani, miyoyo yonse ndi yanga, monga moyo wa atate momwemonso moyo wa mwana, ndiyo yanga; moyo wochimwawo ndiwo udzafa. Koma munthu akakhala wolungama, nakachita chiweruzo ndi chilungamo, wosadya pamapiripo, wosakweza maso ake kumafano a nyumba ya Israele, wosaipsa mkazi wa mnansi wake, kapena kuyandikira mkazi ataoloka, wosasautsa munthu aliyense, koma wambwezera wangongole chigwiriro chake, wosatenga zofunkha, anampatsa wanjala chakudya chake, naveka wamaliseche ndi chovala, wosapereka molira phindu, wosatenga choonjezerapo wobweza dzanja lake lisachite chosalungama, woweruza zoona pakati pa munthu ndi mnzake, amayenda m'malemba anga, nasunga maweruzo anga kuchita chokhulupirika; iye ndiye wolungama, adzakhala ndi moyo ndithu, anena Ambuye Yehova. Akabala mwana ndiye mkhungu, wokhetsa mwazi, wochita chimodzi cha izi, wosachita zabwino zonse zija, koma anadyanso pamapiri, naipsa mkazi wa mnansi wake, nasautsa osauka ndi osowa, natenga zofunkha, wosabwezera chigwiriro, nakweza maso ake kumafano, nachita chonyansa, napereka molira phindu, nalandira choonjezerapo; adzakhala ndi moyo uyu kodi? Sadzakhala ndi moyo, anachita zonyansa izi zonse; kufa adzafadi, mwazi wake umkhalira. Taona tsono, yemweyo akabala mwana uyu, naona zochimwa zonse adazichita atate wake, naopa wosachita zoterezo, wosadya pamapiri, kapena kukweza maso ake kumafano a nyumba ya Israele, wosaipsa mkazi wa mnansi wake, kapena kusautsa wina aliyense, wosatenga chigwiriro, wosatenga zofunkha; koma anapatsa wanjala chakudya chake, naveka wamaliseche ndi chovala, naletsa dzanja lake pa wozunzika, wosalandira phindu kapena choonjezerapo, wochita maweruzo anga, nayenda m'malemba anga; uyu sadzafera mphulupulu ya atate wake, adzakhala ndi moyo ndithu. Atate wake, popeza anazunza chizunzire, nafunkha za mbale wake, nachita chimene sichili chabwino pakati pa anthu ake, taona, adzafa mu mphulupulu yake. Koma inu mukuti, Alekeranji mwana kusenza mphulupulu za atate wake? Mwanayo akachita chiweruzo ndi chilungamo, nakasunga malemba anga onse, ndi kuwachita, adzakhala ndi moyo ndithu. Moyo wochimwawo ndiwo udzafa; mwana sadzasenza mphulupulu za atate wake, ndi atate sadzasenza mphulupulu za mwana; chilungamo cha wolungama chidzamkhalira, ndi choipa cha woipa chidzamkhalira, Koma woipayo akabwerera kusiya machimo ake onse adawachita nakasunga malemba anga onse, ndi kuchita chiweruzo ndi chilungamo, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa. Nnena chimodzi chonse cha zolakwa zake zonse adazichita chidzakumbukika chimtsutse; m'chilungamo chake adachichita adakhala ndi moyo. Ngati ndikondwera nayo imfa ya woipa? Ati Ambuye Yehova, si ndiko kuti abwerere kuleka njira yake, ndi kukhala ndi moyo? Koma wolungamayo akabwerera kuleka chilungamo chake, nakachita mphulupulu, ndi kuchita monga mwa zonyansa zonse azichita woipa, adzakhala ndi moyo kodi? Nnena chimodzi cha zolungama zake zonse adzazichita chidzakumbukika m'kulakwa kwake analakwa nako, ndi m'kuchimwa kwake anachimwa nako; momwemo adzafa. Koma mukuti, Njira ya Ambuye njosayenera. Tamvera tsono nyumba ya Israele, Kodi njira yanga njosayenera? Njira zanu si ndizo zosayenera? Wolungamayo akatembenukira kuleka chilungamo chake, nakachita mphulupulu, adzafa momwemo; m'mphulupulu yake adaichita adzafa. Ndipo woipayo akatembenukira kuleka choipa chake adachichita, nakachita chiweruzo ndi chilungamo, adzapulumutsa moyo wake. Popeza anasamalira, natembenukira kuleka zolakwa zake zonse adazichita, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa. Koma nyumba ya Israele imanena, Njira ya Ambuye njosayenera. Inu, nyumba ya Israele, kodi njira zanga nzosayenera? Njira zanu si ndizo zosayenera? Chifukwa chake ndidzakuweruzani inu, nyumba ya Israele, yense monga mwa njira zake, ati Ambuye Yehova. Bwererani, nimutembenukire kuleka zolakwa zanu zonse, ndipo simudzakhumudwa nazo, ndi kuonongeka nayo mphulupulu. Tayani, ndi kudzichotsera zolakwa zanu zonse zimene munalakwa nazo, ndi kudzifunira mtima watsopano, ndi mzimu watsopano; pakuti mudzaferanji inu, nyumba ya Israele? Pakuti sindikondwera nayo imfa ya wakufayo, ati Ambuye Yehova; chifukwa chake bwererani, nimukhale ndi moyo. Ndipo iwe, takwezera akalonga a Israele nyimbo ya maliro, uziti, Mai wako ndi chiyani? Mkango waukazi unabwanthama mwa mikango, unalera ana ake pakati pa misona. Ndipo unalera mmodzi wa ana ake, iye nasanduka msona, unaphunzira kugwira nyama, unalusira anthu. Mitundu ya anthu idamva mbiri yake, unagwidwa m'mbuna mwao; ndipo anadza nao ndi zokowera kudziko la Ejipito. Pakuona tsono waukaziwo, kuti unalindirira, ndi kuti chiyembekezo chake chidatha, unatenga wina wa ana ake, numsandutsa msona. Ndipo unayendayenda pakati pa mikango, nukhala msona, nuphunzira kugwira nyama, nulusira anthu. Ndipo unadziwa amasiye ao, nupasula midzi yao, ndipo dziko ndi kudzala kwake linasanduka labwinja, chifukwa cha phokoso la kubangula kwake. Pamenepo mitundu ya anthu inadzipereka kuukola kuchokera kumaiko a kumbali zonse, niuphimba ndi ukonde wao, nugwidwa uwu m'mbuna mwao. Nauika m'chitatanga ndi zokowera, nadza nao kwa mfumu ya ku Babiloni; anaulonga m'malinga, kuti mau ake asamvekenso pa mapiri a Israele. Mai wako ananga mpesa wookedwa kumadzi; muja anakhala mumtendere unabala zipatso, wodzala ndi nthambi, chifukwa cha madzi ambiri. Ndipo unali nazo ndodo zolimba zikhale ndodo zachifumu, za ochita ufumu, ndi msinkhu wao unakula kufikira kumitambo, nizinaoneka m'kusomphoka kwao pakati pa nthambi zake zambiri. Koma unazulidwa mwaukali, unaponyedwa pansi ndi mphepo ya kum'mawa, inaumitsa zipatso zake, ndodo zake zolimba zinathyoka ndi kuuma, moto unazitha. Ndipo tsopano waokedwa m'chipululu m'dziko louma ndi la ludzu. Unatulukanso moto kundodo za kunthambi zake, unatha zipatso zake; m'mwemo ulibe ndodo yolimba ikhale ndodo yachifumu ya kuchita ufumu. Iyi ndi nyimbo idzakhala nyimbo ya maliro. Ndipo kunali chaka chachisanu ndi chiwiri, mwezi wachisanu, tsiku lakhumi la mwezi, anadza akulu ena a Israele kufunsira kwa Yehova, nakhala pansi iwowa pamaso panga. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe lankhula ndi akulu a Israele, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Mwadza kodi kufunsira kwa Ine? Pali Ine, sindidzafunsidwa ndi inu, ati Ambuye Yehova. Udzawaweruza kodi, wobadwa ndi munthu iwe? Udzawaweruza? Uwadziwitse zonyansa za makolo ao, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Tsiku lija ndinamsankha Israele, ndi kukwezera mbeu ya nyumba ya Yakobo dzanja langa, ndi kudzidziwitsa kwa iwo m'dziko la Ejipito, pakuwakwezera dzanja langa, ndi kuti, Ine ndine Yehova Mulungu wanu; tsiku lomwelo ndinawakwezera dzanja langa kuwatulutsa m'dziko la Ejipito, kunka nao kudziko ndinawazondera, moyenda mkaka ndi uchi, ndilo lokometsetsa mwa maiko onse; ndipo ndinanena nao, Aliyense ataye zonyansa za pamaso pake, nimusadzidetsa ndi mafano a Ejipito; Ine ndine Yehova Mulungu wanu. Koma anapandukira Ine, osafuna kundimvera Ine, sanataye yense zonyansa pamaso pake, sanaleke mafano a Ejipito; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'dziko la Ejipito. Koma ndinachichita chifukwa cha dzina langa, kuti lisadetsedwe pamaso pa amitundu amene anakhala pakati pao, amene pamaso pao ndinadzidziwitsa kwa iwo, pakuwatulutsa m'dziko la Ejipito. Momwemo ndinatuluka nao m'dziko la Ejipito, ndi kulowa nao kuchipululu. Ndinawapatsanso malemba anga, ndi kuwadziwitsa maweruzo anga, ndiwo munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo. Ndipo ndinawapatsanso masabata anga akhale chizindikiro pakati pa Ine ndi iwo, kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova wakuwapatula. Koma nyumba ya Israele inapandukira Ine m'chipululu, sanayende m'malemba anga, nanyoza maweruzo anga, amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo; ndi masabata anga anawaipsa kwambiri; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga m'chipululu kuwatha. Koma ndinachichita chifukwa cha dzina langa, kuti lisaipsidwe pamaso pa amitundu amene ndinawatulutsa pamaso pao. Ndipo ndinawakwezeranso dzanja langa m'chipululu, kusawalowetsa m'dzikolo ndidawapatsa, moyenda mkaka ndi uchi, ndilo lokometsetsa mwa maiko onse; popeza ananyoza maweruzo anga, osayenda m'malemba anga, naipsa masabata anga; pakuti mitima yao inatsata mafano ao. Koma diso langa lidawaleka osawaononga, sindinawatha onse m'chipululu. Ndipo ndinati kwa ana ao m'chipululu, Musamayenda m'malemba a atate anu, musawasunga maweruzo ao, kapena kudzidetsa ndi mafano ao; Ine ndine Yehova Mulungu wanu, muziyenda m'malemba anga, ndi kusunga maweruzo anga, ndi kuwachita; muzipatulanso masabata anga, ndipo adzakhala chizindikiro pakati pa Ine ndi inu, kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu. Koma anawo anapandukira Ine, sanayende m'malemba anga, kapena kusunga maweruzo anga kuwachita, amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo; anaipsa masabata anga; pamenepo ndinati ndidzawatsanulira ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'chipululu. Koma ndinabweza dzanja langa ndi kuchichita, chifukwa cha dzina langa; kuti lisaipsidwe pamaso pa amitundu, amene ndinawatulutsa pamaso pao. Ndinawakwezeranso dzanja langa m'chipululu, kuti ndidzawabalalitsa mwa amitundu, ndi kuwamwaza m'maiko; popeza sanachite maweruzo anga, koma ananyoza malemba anga, naipsa masabata anga, ndi maso ao anatsata mafano a atate ao. Momwemonso ndinawapatsa malemba amene sanali abwino, ndi maweruzo osakhala nao ndi moyo; ndinawadetsanso m'zopereka zao; pakuti anapititsa pamoto onse oyamba kubadwa kuti ndiwapasule; kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova. Chifukwa chake wobadwa ndi munthu iwe, lankhula ndi nyumba ya Israele, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Mwa ichinso atate anu anandichitira mwano pakundilakwira Ine. Nditafika nao m'dzikolo ndinawakwezera dzanja langa kuwapatsa ilo, anapenya chitunda chilichonse chachitali, ndi mtengo uliwonse wagudugudu, naphera pomwepo nsembe zao, naperekapo nsembe zao zondiputa, aponso anachita fungo lao lokoma, nathiraponso nsembe zao zothira. Pamenepo ndinanena nao, Msanje wotani uwu mumapitako? Momwemo dzina lake litchedwa Msanje, mpaka lero lino. Chifukwa chake uziti kwa nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Mudzidetsa kodi monga umo anachitira makolo anu? Muchita chigololo kodi kutsata zonyansa zao? Ndipo popereka zopereka zanu popititsa ana anu pamoto, mudzidetsa kodi ndi mafano anu onse mpaka lero lino? Ndipo kodi ndidzafunsidwa ndi inu, nyumba ya Israele? Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindidzafunsidwa ndi inu; ndi ichi chimauka mumtima mwanu sichidzachitika, umo mukuti, Tidzakhala ngati amitundu, ngati mabanja a m'maiko, kutumikira mtengo ndi mwala. Pali Ine, ati Ambuye Yehova, zedi ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi ukali wotsanulidwa, ndidzakhala mfumu yanu. Ndipo ndidzakutulutsani mwa mitundu ya anthu, ndi kukusonkhanitsani m'maiko munabalalikamo ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi ukali wotsanulidwa. Ndipo ndidzalowa nanu m'chipululu cha mitundu ya anthu, ndi kukuweruzani komweko popenyana maso. Monga ndinaweruza makolo anu m'chipululu cha dziko la Ejipito, momwemo ndidzaweruza inu, ati Ambuye Yehova. Ndipo ndidzakupititsani pansi pa ndodo ya mbusa ndi kukulowetsani m'chimango cha chipangano; ndipo ndidzasankhula mwa inu opanduka ndi ondilakwira, ndidzawatulutsa m'dziko logoneramo iwo; koma sadzalowa m'dziko la Israele; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Ndipo inu, nyumba ya Israele, atero Ambuye Yehova, mukani, tumikirani yense mafano ake, ndi m'tsogolo momwe, popeza simundimvera Ine; koma musaipsanso dzina langa lopatulika ndi zopereka zanu ndi mafano anu. Pakuti pa phiri langa lopatulika, pa phiri lothuvuka la Israele, ati Ambuye Yehova, pomwepo onse a nyumba ya Israele, onsewo adzanditumikira Ine m'dzikomo; pomwepo ndidzawalandira, ndi pomwepo ndidzafuna nsembe zanu zokweza, ndi zoyamba za msonkho wanu, pamodzi ndi zopatulika zanu zonse. Ngati fungo lokoma ndidzakulandirani pakukutulutsani mwa mitundu ya anthu, ndipo ndidzakusonkhanitsani kukuchotsani m'maiko munabalalikiramo, ndipo ndidzazindikirika Woyera mwa inu pamaso pa amitundu. Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakukulowetsani Ine m'dziko la Israele, m'dzikoli ndinalikwezera dzanja langa kulipereka kwa makolo anu. Ndi pomwepo mudzakumbukira njira zanu, ndi zonse mudazichita ndi kudzidetsa nazo, ndipo mudzakhala onyansa pamaso pa inu nokha, chifukwa cha zoipa zanu zonse mudazichita. M'mwemo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova nditachita nanu chifukwa cha dzina langa, si monga mwa njira zanu zoipa, kapena monga mwa machitidwe anu ovunda, nyumba ya Israele inu, ati Ambuye Yehova. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako njira ya kumwera, nubenthulire mau kumwera, nunenere nkhalango ya kuthengo la kumwera kwa Yuda; nuziti kwa nkhalango ya kumwera kwa Yuda, Tamvera mau a Yehova, Atero Ambuye Yehova, Taona ndidzayatsa moto mwa iwe, udzanyeketsa mtengo uliwonse wauwisi mwa iwe, ndi mtengo uliwonse wouma; malawi amoto sadzazimika, ndi nkhope zonse kuyambira kumwera kufikira kumpoto zidzapsa nao. Ndi anthu onse adzaona kuti Ine Yehova ndinauyatsa, sudzazimika. Pamenepo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! Anandinena, Wonena mafanizo uyu. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako ku Yerusalemu, nuwabenthulire mau malo opatulikawa, nunenere dziko la Israele kulitsutsa; nuziti kwa dziko la Israele, Atero Yehova, Taona Ine ndine wotsutsana nawe, ndidzasolola lupanga langa m'chimake, ndi kukulikhira olungama ndi oipa. Popeza ndidzakulikhira olungama ndi oipa, chifukwa chake lupanga langa lidzasololokera anthu onse, kuyambira kumwera kufikira kumpoto; ndi anthu onse adzadziwa kuti Ine Yehova ndasolola lupanga langa m'chimake, silidzabwereranso. Koma wobadwa ndi munthu iwe, usa moyo, ndi kuduka msana, ndi kuwawa mtima, uuse moyo pamaso pao. Ndipo kudzakhala akanena ndi iwe, Uusa moyo chifukwa ninji? Uzikati, Chifukwa cha mbiri; pakuti ikudza, ndi mtima uliwonse udzasungunuka, ndi manja onse adzalenda, ndi mzimu uliwonse udzakomoka, ndi maondo onse adzaweyeseka ngati madzi; taona ilinkudza, inde idzachitika, ati Ambuye Yehova. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, nenera ndi kuti, Atero Yehova, Nena, Lupanga, lupanga lanoledwa, latuulidwanso; lanoledwa kuti liphetu, lituulidwa kuti linge mphezi; tisekererepo kodi? Ndilo ndodo yachifumu ya mwana wanga, yopeputsa mtengo uliwonse. Ndipo analipereka alituule, kuti achite nalo lupangali analinola, inde analituula kulipereka m'dzanja la wakupha. Fuula ndi kulira, wobadwa ndi munthu iwe, pakuti likhalira pa anthu anga, likhalira pa akalonga onse a Israele, laperekedwa kulupanga pamodzi ndi anthu anga; chifukwa chake panda pantchafu pako. Pakuti pali kuyesedwa; ndipo nanga ndodo yachifumu yopeputsa ikapanda kukhalanso? Ati Ambuye Yehova. Ndipo wobadwa ndi munthu iwe, nenera, nuombe manja, lupanga lipitilize katatu, lupanga la wolasidwa ndilo lupanga la wolasidwa wamkuluyo, limene liwazinga. Ndalozetsa nsonga ya lupanga kuzipata zao zonse, kuti mtima wao usungunuke, ndi kukhumudwa kwao kuchuluke; ha! Analituula linyezimire, analisongoza liphe. Udzisonkhanitsire pamodzi, muka kudzanja lamanja; undandalitsa nkhondo kumuka kulamanzere; kulikonse ilozako nkhope yako. Inenso ndidzaomba manja anga, ndipo ndidzakukwaniritsa ukali wanga; Ine Yehova ndanena. Ndipo mau a Yehova anandidzera, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, udziikire njira ziwiri zodzera lupanga la mfumu ya ku Babiloni; zonse ziwiri zichokere dziko lomwelo; nulembe chizindikiro cholozera, uchilembe pa mphambano ya njira ya kumudzi. Uiike njira yodzera lupanga kunka ku Raba wa ana a Amoni, ndi ya ku Yuda ku Yerusalemu, mudzi walinga. Pakuti mfumu ya ku Babiloni aima pa mphambano ya njira, polekana njira ziwirizo, kuti aombeze maula; agwedeza mivi, afunsira kwa aterafi, apenda ndi chiwindi. M'dzanja lake lamanja muli ula wa ku Yerusalemu, kuika zogundira, kutsegula pakamwa pa kupha, kukweza mau ndi kufuula, kuikira zitseko zogundira, kuundira mtumbira, kumanga malinga. Ndipo kudzakhala ngati kuombeza konyenga pamaso pa iwo amene anawalumbirira malumbiro; koma akumbutsa mphulupulu kuti akodwe. Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza mwakumbutsa mphulupulu yanu povumbuluka zolakwa zanu, kotero kuti machimo anu aoneka m'zonse muzichita, popeza mukumbukika, mudzagwidwa ndi dzanja. Ndipo iwe wolasidwa woipa, kalonga wa Israele, amene lafika tsiku lako, nthawi ya mphulupulu yotsiriza; atero Ambuye Yehova, Chotsa chilemba, vula korona, ufumu sudzakhalanso momwemo, kweza chopepuka, chepsa chokwezeka. Ndidzagubuduzagubuduza ufumu uno, sudzakhalanso kufikira akadza Iye mwini chiweruzo; ndipo ndidzaupereka kwa Iye. Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, nenera, nuziti, Atero Ambuye Yehova za ana a Amoni, ndi za chitonzo chao; nuziti, Lupanga, lupanga lasololedwa, latuulidwa, kuti likaphe, kuti liononge, likhale lonyezimira. Akuonera zopanda pake, akuombezera mabodza, lupanga likugoneka pa makosi a oipa olasidwa, amene lafika tsiku lao nthawi ya mphulupulu yotsiriza. Ulibwezere m'chimake. Pamalo unalengedwapo m'dziko la kubadwa kwako ndidzakuweruza. Ndipo ndidzakutsanulira mkwiyo wanga, ndidzakuuzira ndi moto wa kuzaza kwanga, ndidzakuperekanso m'manja mwa anthu ankharwe odziwa kuononga. Udzakhala ngati nkhuni ya pamoto, mwazi wako udzakhala pakati pa dziko, sudzakumbukikanso; pakuti Ine ndine Yehova ndachinena. Anandidzeranso mau a Yehova, akuti, Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, udzaweruza, udzauweruza mudziwo wa mwazi kodi? Uudziwitse tsono zonyansa zake zonse. Nuziti, Atero Ambuye Yehova, Ndiwo mudzi wokhetsa mwazi pakati pake kuti nthawi yake ifike, nudzipangire mafano udzidetsa nao. Wapalamula nao mwazi wako, waukhetsa, nudetsedwa nao mafano ako udawapanga, nuyandikizitsa masiku ako, wafikiranso zakozako; chifukwa chake ndakuika ukhale chitonzo cha amitundu ndi choseketsa cha maiko onse. Okhala pafupi ndi okhala patali adzakuseka pwepwete, wodetsedwa dzina iwe, wodzala ndi kusokosera. Taona akalonga a Israele, yense monga mwa mphamvu yake, akhala mwa iwe, kuti akhetse mwazi. Mwa iwe anapepula atate ndi mai, pakati pa iwe anamchitira mlendo momzunza, mwa iwe anazunza ana amasiye, ndi mkazi wamasiye. Wanyoza zopatulika zanga, waipsa masabata anga. Anthu oneneza anali mwa iwe, kuti akhetse mwazi; ndipo anadya pamapiri mwa iwe, pakati pa iwe anachita zamanyazi. Anavula umaliseche wa atate ao mwa iwe, mwa iwe anachepsa wodetsedwa ndi kooloka kwake. Ndipo wina anachita chonyansa ndi mkazi wa mnansi wake, winanso wadetsa mpongozi wake mwamanyazi, ndi wina mwa iwe anaipitsa mlongo wake mwana wamkazi wa atate wake. Analandira mphotho mwa iwe kukhetsa mwazi, walandira phindu loonjezerapo, wanyengerera anansi ako ndi kuwazunza, ndipo wandiiwala Ine, ati Ambuye Yehova. Taona, ndaomba manja pa phindu lako lonyenga waliona, ndi pa mwazi wokhala pakati pako. Mtima wako udzaimika kodi, manja ako adzalimbikira masikuwo ndidzachita nawe? Ine Yehova ndanena, ndidzachichita. Ndipo ndidzakumwaza mwa amitundu, ndi kukubalalitsa m'maiko, ndi kukuthera zodetsa zako zikuchokere. Ndipo udzaipsidwa mwa iwe wekha pamaso pa amitundu; motero udzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Ndipo mau a Yehova anandidzera, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, nyumba ya Israele yandikhalira mphala; onsewo ndiwo mkuwa, ndi seta, ndi chitsulo, ndi ntovu, m'kati mwa ng'anjo; ndiwo mphala zasiliva. Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza mwasanduka mphala nonsenu, chifukwa chake taonani, ndidzakusonkhanitsani m'kati mwa Yerusalemu. Monga asonkhanitsa mtapo wa siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, ndi ntovu, ndi seta, m'kati mwa ng'anjo, kuzivukutira moto, kuzisungunula momwemo, ndidzakusonkhanitsani mu mkwiyo wanga ndi ukali wanga, ndi kukuikani komweko, ndi kukusungunulani. Inde ndidzakusonkhanitsani, ndi kukuvukutirani ndi moto wa kuzaza kwanga, ndipo mudzasungunuka pakati pake. Monga siliva asungunuka m'kati mwa ng'anjo, momwemo inu mudzasungunuka m'kati mwake; motero mudzadziwa kuti Ine Yehova ndakutsanulirani ukali wanga. Nandidzeranso mau a Yehova, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, nena ndi Yuda, Iwe ndiwe dziko losayeretsedwa, losavumbwa mvula tsiku la ukalilo. Pali chiwembu cha aneneri ake pakati pake, ngati mkango wobangula womwetula nyama, analusira miyoyo, alanda chuma ndi za mtengo wake, achulukitsa amasiye pakati pake. Ansembe ake achitira choipa chilamulo changa, nadetsa zopatulika zanga, sasiyanitsa pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba, ndipo sazindikiritsa anthu pakati pa zodetsa ndi zoyera, nabisira masabata anga maso ao; ndipo Ine ndidetsedwa pakati pao. Akalonga ake m'kati mwake akunga mimbulu yakumwetula nyama, kukhetsa mwazi, kuononga miyoyo, kuti aone phindu lonyenga. Ndipo aneneri ao anawamatira ndi dothi losapondeka, ndi kuonera zopanda pake, ndi kuwaombezera mabodza, ndi kuti, Atero Ambuye Yehova, posanena Yehova. Anthu a m'dziko anazunzazunza, nalandalanda mwachiwawa, napsinja ozunzika ndi aumphawi, nazunza mlendo wopanda chifukwa. Ndipo ndinafunafuna munthu pakati pao wakumanganso linga, ndi kuimira dziko popasukira pamaso panga, kuti ndisaliononge; koma ndinapeza palibe. Chifukwa chake ndinawatsanulira ukali wanga, ndawatha ndi moto wa kuzaza kwanga, njira yaoyao ndinaibweza pa mutu pao, ati Ambuye Yehova. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, panali akazi awiri, mai wao ndi mmodzi; ndipo anachita chigololo iwo m'Ejipito, anachita chigololo m'ubwana wao; pomwepo anthu anasindikiza mawere ao, pomweponso anakhudza nsonga za mawere za unamwali wao. Ndipo maina ao ndiwo Ohola wamkulu, ndi Oholiba mng'ono wake; nakhala anga, nabala ana aamuna ndi aakazi. Ndipo maina ao, Samariya ndiye Ohola, ndi Yerusalemu ndiye Oholiba. Koma Ohola anachita chigololo pamene anali wanga, anaumirira mabwenzi ake Aasiriya oyandikizana naye; ovala chibakuwa, ziwanga, ndi akazembe, onsewo anyamata ofunika, anthu oyenda pa akavalo. Ndipo anachita nao zigololo zake, ndiwo anthu osankhika a ku Asiriya onsewo, ndipo ali onse anawaumirira anadziipsa nao mafano ao. Sanalekenso zigololo zake zochokera ku Ejipito, pakuti anagona naye m'unamwali wake, nakhudza mawere a unamwali wake, namtsanulira chigololo chao. Chifukwa chake ndampereka m'dzanja la mabwenzi ake, m'dzanja la Aasiriya amene anawaumirira. Iwowa anavula umaliseche wake, anatenga ana ake aamuna ndi aakazi, namupha iyeyu ndi lupanga; ndi dzina lake linamveka mwa akazi atamchitira maweruzo. Pamene mng'ono wake Oholiba anachiona, anavunda ndi kuumirira kwake koposa iyeyo; ndi zigololo zake zidaposa zigololo za mkulu wake. Anaumirira Aasiriya, ziwanga, ndi akazembe oyandikizana naye, ovala zangwiro, anthu oyenda pa akavalo, onsewo anyamata ofunika. Ndipo ndinamuona kuti anadetsedwa, onse awiri adatenga njira yomweyi. Ndipo anaonjeza zigololo zake, naona amuna olembedwa pakhoma, zithunzithunzi za Ababiloni olembedwa ndi kundwe; omangira malamba m'chuuno mwao, ndi nduwira zazikulu zonika pamitu pao, maonekedwe ao ngati akalonga onsewo, akunga a ku Babiloni, dziko la kubadwa kwao ndi Kasidi. Ndipo pakuwaona anawalakalaka, nawatumira mithenga kudziko la Ababiloni. Namdzera a ku Babiloni ku kama wa chikondi, namdetsa ndi chigololo chao, iyenso anadetsedwa nao; atatero moyo wake unafukidwa nao. M'mwemo iye anawulula chigololo chake, navula umaliseche wake; pamenepo moyo wanga unaipidwa naye, monga umo moyo unaipidwira mkulu wake. Koma anachulukitsa zigololo zake, nakumbukira masiku a ubwana wake, muja anachita chigololo m'dziko la Ejipito. Ndipo anaumirira amuna ao amene nyama yao ikunga ya abulu, ndi kutentha kwao ngati kutentha kwa akavalo. Momwemo wautsanso choipa cha ubwana wako, pakukhudza Aejipito nsonga za mawere ako, chifukwa cha mawere a ubwana wako. Chifukwa chake, Oholiba, atero Ambuye Yehova, Taona ndidzakuutsira mabwenzi ako amene moyo wako wakufidwa nao, ndi kukufikitsira iwowa pozungulira ponse atsutsane nawe, a ku Babiloni, ndi Ababiloni, Pekodi, ndi Sowa, ndi Kowa, ndi Aasiriya onse pamodzi nao, anyamata ofunika, ziwanga ndi akazembe onsewo, akalonga ndi mandoda onsewo, oyenda ndi akavalo. Ndipo adzakudzera ndi zida, magaleta a nkhondo, ndi magaleta ena, pamodzi ndi msonkhano wa mitundu ya anthu; adzadziikira pozungulira pako ndi zikopa zotchinjiriza ndi zisoti; ndipo ndidzawaika aweruze, nadzakuweruza monga mwa maweruzo ao. Ndipo ndidzakuikira nsanje yanga, nadzakuchitira mwaukali, iwowa adzakudula mphuno ndi makutu; ndi otsiriza ako adzagwa ndi lupanga, adzakuchotsera ana ako aamuna ndi aakazi, ndi otsirizira ako adzatha ndi moto. Adzakuvulanso zovala zako, ndi kukuchotsera zokometsera zako zokongola. Motero ndidzakuleketsera choipa chako, ndi chigololo chako chochokera m'dziko la Ejipito; ndipo sudzazikwezeranso maso ako, kapena kukumbukiranso Ejipito. Pakuti atero Ambuye Yehova, Taona ndidzakupereka m'dzanja la iwo amene uwada, m'dzanja la iwo amene moyo wako ufukidwa nao; ndipo adzachita nawe mwaudani, nadzalanda zonse udazigwirira ntchito, nadzakusiya wamaliseche ndi wausiwa; ndi umaliseche wa zigololo zako udzavulidwa, dama lako ndi zigololo zako zomwe. Izi adzakuchitira chifukwa watsata amitundu, ndi kuchita nao chigololo, popezanso wadetsedwa ndi mafano ao. Wayenda m'njira ya mkulu wako, chifukwa chake ndidzapereka chikho chake m'dzanja lako. Atero Ambuye Yehova, M'chikho cha mkulu wako udzamweramo ndicho chachikulu ngati mchenje; adzakuseka pwepwete, nadzakunyoza muli zambiri m'menemo. Udzadzala ndi kuledzera ndi chisoni, ndi chikho chodabwitsa ndi cha chipasuko, ndi chikho cha mkulu wako Samariya. Udzamwa ichi ndi kugugudiza, ndi kuchechetachecheta zibade zake, ndi kung'amba mawere ako; pakuti ndachinena, ati Ambuye Yehova. Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza wandiiwala Ine, ndi kunditaya pambuyo pako, uzisenza iwenso choipa chako ndi zigololo zako. Ndipo Yehova anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, kodi udzaweruza Ohola ndi Oholiba? Uwafotokozere tsono zonyansa zao. Pakuti anachita chigololo, ndi m'manja mwao muli mwazi, ndipo anachita chigololo ndi mafano ao, nawapititsiranso pamoto ana ao amuna amene anandibalira, kuti athedwe. Anandichitiranso ichi, anadetsa malo anga opatulika tsiku lomwelo, naipsa masabata anga; pakuti ataphera mafano ao, ana ao analowa tsiku lomwelo m'malo anga opatulika kuwadetsa; ndipo taona, anatero m'kati mwa nyumba yanga. Ndiponso munatuma kuitana anthu ochokera kutali, ndiwo munawatumira mthenga; ndipo taona, anadza amenewo unasamba, chifukwa cha iwo unapaka maso ako mankhwala, ndi kuvala zokometsera; ndipo unakhala pa kama waulemu, pali gome lokonzekeratu patsogolo pake; pamenepo unaika chofukiza chonga ndi mafuta anga. Ndipo phokoso lalikulu lidaleka pomwepo, ndipo pamodzi ndi anthu wamba anabwera nao olodzera ochokera kuchipululu, naika makoza m'manja mwa awiriwo, ndi akorona okongola pamitu pao. Pamenepo ndinati za uyu anakalamba nazo zigololo, Tsopano iwo adzachita zigololo naye, ndi iyenso nao. Ndipo analowa kwa iye monga umo amalowera kwa mkazi wachigololo, motero analowa kwa Ohola ndi Oholiba akazi oipawo. Ndipo anthu olungama adzawaweruza monga mwa maweruzo a achigololo, ndi maweruzo akazi okhetsa mwazi; pakuti ndiwo achigololo, ndi m'manja mwao muli mwazi. Pakuti atero Ambuye Yehova, Ndidzawakweretsera msonkhano wa anthu, ndi kuwapereka awazunze, ndi kulanda chuma chao. Ndi msonkhanowo udzawaponya miyala, ndi kuwatha ndi malupanga ao, adzawapha ana ao aamuna ndi aakazi, ndi kutentha nyumba zao ndi moto. Momwemo ndidzaleketsa dama m'dzikomo, kuti alangizidwe akazi onse kusachita monga mwa dama lanu. Ndipo adzakubwezerani dama lanu, nimudzasenza machimo a mafano anu; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova. Anandidzeranso mau a Yehova chaka chachisanu ndi chinai, mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, ndi kuti, Wobadwa ndi munthu iwe, Udzilembere dzina la tsiku lomwe lino, mfumu ya ku Babiloni wayandikira Yerusalemu tsiku lomwe lino. Ndipo uphere nyumba yopandukayo fanizo, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Tereka mphika; uutereke, nuthire madzi m'menemo. Longamo pamodzi ziwalo zake, ziwalo zonse zokoma, mwendo wathako ndi wamwamba; uudzaze ndi mafupa osankhika. Tengako choweta chosankhika, nuikire mafupa mulu wa nkhuni pansi; ubwadamuke, ndi mafupa ake omwe uwaphike m'mwemo. Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Tsoka mudzi wokhetsa mwazi, mphika m'mene muli dzimbiri, losauchokera dzimbiri lake; uchotsemo chiwalochiwalo; sanaugwere maere. Pakuti mwazi wake uli m'kati mwake anauika pathanthwe poyera, sanautsanulire panthaka kuukwirira ndi fumbi. Pofuna kuutsa ukali, ndi kubwezera chilango, ndaika mwazi wake pathanthwe poyera, kuti usakwiririke. Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Tsoka mudzi wokhetsa mwazi, ndidzakulitsa mulu wa nkhuni. Zichuluke nkhuni, koleza moto, nyama ipse, uwiritse msuzi wake, ubwadamuke, ndi mafupa ake atibuke. Pamenepo uukhazike pa makala ake opanda kanthu m'menemo, kuti utenthe, nuyake mkuwa wake; ndi kuti chodetsa chake chisungunuke m'mwemo, kuti dzimbiri lake lithe. Ntchito ya mphika ndi yolemetsa, koma dzimbiri lake lalikulu siliuchokera, dzimbiri lake liyenera kumoto. M'chodetsa chako muli dama, popeza ndinakuyeretsa; koma sunayeretsedwa, sudzayeretsedwanso kukuchotsera chodetsa chako, mpaka nditakwaniritsa ukali wanga pa iwe. Ine Yehova ndachinena, chidzachitika; ndipo ndidzachichita, sindidzamasula, kapena kulekerera, kapena kuwaleka, monga mwa njira zako, ndi monga umo unachitira adzakuweruza iwe, ati Ambuye Yehova. Mau a Yehova anandidzeranso, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, taona, ndikuchotsera chokonda maso ako ndi chikomo, koma usamve chisoni, kapena kulira, kapena kudza misozi. Usa moyo mosamveka, usalira wakufayo, dzimangire chilemba, nuvale nsapato kumapazi ako, usaphimbe milomo yako. Kapena kudya mkate wa anthu. Ndipo nditalankhula ndi anthu m'mawa, madzulo ake mkazi wanga anamwalira; ndi m'mawa mwake ndinachita monga anandilamulira. Nanena nane anthu, Simudzatiuza kodi zitani nafe izi muzichita? Ndipo ndinanena nao, Anandidzera mau a Yehova, akuti, Nena ndi nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Taona, ndidzadetsa malo anga opatulika, ulemerero wa mphamvu yanu, chokonda m'maso mwanu, chimene moyo wanu ali nacho chifundo; ndipo ana anu aamuna ndi aakazi otsalira inu adzagwa ndi lupanga. Ndipo mudzachita monga umo ndachitira ine, osaphimba milomo yanu, kapena kudya mkate wa anthu. Ndi zilemba zanu zidzakhala pamitu panu, ndi nsapato zanu kumapazi anu, simudzachita chisoni kapena kulira, koma mudzaonda ndi mphulupulu zanu, ndi kubulirana wina ndi mnzake. Momwemo Ezekiele adzakhala kwa inu chizindikiro; umo monse anachitira iye mudzachita ndinu; chikadza ichi mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova. Ndipo wobadwa ndi munthu iwe, sikudzakhala kodi tsiku loti ndiwachotsera mphamvu yao, chimwemwe chao chopambana, chowakonda m'maso mwao, ndi chokhumbitsa mtima wao, ana ao aamuna ndi aakazi, kuti tsiku lomwelo wopulumukayo adzakudzera, kukumvetsa m'makutu mwako? Tsiku lomwelo pakamwa pako padzatsegukira wopulumukayo; mudzalankhula osakhalanso chete, momwemo udzawakhalira chizindikiro; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Ndipo mau a Yehova anandidzera, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, Lozetsa nkhope yako kwa ana a Amoni, nuwanenere; nunene kwa ana a Amoni, Tamverani mau a Ambuye Yehova, Atero Ambuye Yehova, Popeza unati, Onyo, kunena malo anga opatulika; muja anadetsedwa ndi kunena dziko la Israele; muja linapasuka ndi kunena nyumba ya Yuda; muja adalowa kundende; chifukwa chake taona, ndidzakupereka kwa ana a kum'mawa ukhale waowao, kuti amange misasa yao mwa iwe, namange pokhala pao mwa iwe, iwo adzadya zipatso zako ndi kumwa mkaka wako. Ndipo ndidzayesa Raba khola la ngamira, ndi ana a Amoni popumula zoweta zazing'ono; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Pakuti atero Ambuye Yehova, Waomba manja, ndi kuvina, ndi kukondwera ndi chipeputso chonse cha moyo wako, kupeputsa dziko la Israele, chifukwa chake taona, ndakutambasulira dzanja langa, ndipo ndidzakupereka ukhale chofunkha cha amitundu, ndi kukudula mwa mitundu ya anthu, ndi kukutayikitsa m'maiko, ndidzakuononga; motero udzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Atero Ambuye Yehova, Popeza Mowabu ndi Seiri akuti, Taona nyumba ya Yuda ikunga amitundu onse; chifukwa chake taona ndidzatsegula pambali pake pa Mowabu kuyambira kumidzi, kumidzi yake yokhala mphepete, yokometsetsa ya m'dziko, Beteyesimoti, Baala-Meoni, ndi Kiriyataimu, kuwapereka kwa ana a kum'mawa pamodzi ndi ana a Amoni; ndipo ndidzawapereka akhale aoao, kuti ana a Amoni asakumbukikenso mwa amitundu; ndipo ndidzakwaniritsa maweruzo m'Mowabu; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Atero Ambuye Yehova, Popeza Edomu anachita mobwezera chilango pa nyumba ya Yuda, napalamula kwakukulu pakuibwezera chilango, chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Ndidzatambasulira Edomu dzanja langa, ndi kulilikhira munthu ndi nyama, ndi kulisandutsa labwinja; kuyambira ku Temani mpaka Dedani adzagwa ndi lupanga. Ndipo ndidzalibwezera Edomu chilango mwa dzanja la anthu anga Israele; ndipo adzachita m'Edomu monga mwa mkwiyo wanga, ndi ukali wanga; motero adzadziwa kubwezera chilango kwanga, ati Ambuye Yehova. Atero Ambuye Yehova, Popeza Afilisti anachita mobwezera chilango nabwezera chilango ndi mtima wopeputsa kuononga, ndi udani wosatha, chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona ndidzatambasulira Afilisti dzanja langa, ndi kulikha Akereti, ndi kuononga otsalira mphepete mwa nyanja. Ndipo ndidzawabwezera chilango chachikulu, ndi malango ankharwe; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuwabwezera chilango Ine. Ndipo kunali chaka chakhumi ndi chimodzi, tsiku loyamba la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, popeza Tiro ananyodola Yerusalemu, ndi kuti, Onyo, wathyoka uwu udali chipata cha mitundu ya anthu; wanditembenukira ine; ndidzakhuta ine, wapasuka uwu; chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona ndikutsutsa iwe, Tiro, ndidzakukweretsera amitundu, monga nyanja iutsa mafunde ake. Ndipo adzagumula malinga a Tiro, ndi kugwetsa nsanja zake; inde ndidzausesa fumbi lake, ndi kuuyesa pathanthwe poyera. Udzakhala poyanika khoka pakati pa nyanja, pakuti Ine ndachinena, ati Ambuye Yehova; ndipo udzakhala chofunkha cha amitundu. Ndi ana ake akazi okhala kumunda adzaphedwa ndi lupanga; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Pakuti atero Ambuye Yehova, Taona ndidzafikitsira Tiro Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mfumu ya mafumu, yochokera kumpoto ndi akavalo, ndi magaleta, ndi apakavalo, ndi msonkhano wa anthu ambiri. Ana ako akazi adzawapha kumunda ndi lupanga; ndipo adzakumangira nsanja, ndi kukuundira mtumbira, ndi kukuimikira chikopa. Nadzaikira malinga ako zogumulira, nadzagwetsa nsanja zako ndi zida zake. Popeza achuluka akavalo ake, fumbi lao lidzakukuta; malinga ako adzagwedezeka ndi phokoso la apakavalo, ndi njinga za magaleta, polowa iye pa zipata zako, monga umo amalowera m'mudzi popasukira linga lake. Ndi ziboda za akavalo ake iye adzapondaponda m'makwalala ako onse; adzapha anthu ako ndi lupanga; ndi zoimiritsa za mphamvu yako zidzagwa pansi. Ndipo adzalanda chuma chako ndi kufunkha malonda ako, nadzagwetsa malinga ako ndi kupasula nyumba zako zofunika, nadzaponya miyala yako, ndi mitengo yako, ndi fumbi lako, m'madzi. Ndipo ndidzaleketsa phokoso la nyimbo zako, ndi kulira kwa mazeze ako sikudzamvekanso. Ndipo ndidzakuyesa pathanthwe poyera; udzakhala poyanika khoka, sadzakumanganso; pakuti Ine Yehova ndachinena, ati Ambuye Yehova. Atero Ambuye Yehova kwa Tiro, Zisumbu sizidzagwedezeka nanga pomveka kugwa kwako, pobuula olasidwa, pakuchitika kuphako pakati pako? Pamenepo akalonga onse a kunyanja adzatsika ku mipando yachifumu yao, nadzavula zovala zao zopikapika, nadzavala kunjenjemera, nadzakhala panthaka pansi, nadzanjenjemera mphindi zonse ndi kudabwa nawe. Ndipo adzakukwezera nyimbo ya maliro, ndi kunena nawe, Watayika bwanji, ndiwe pokhala pa anthu a panyanja, mudzi womveka, unalimbika panyanja, uwo ndi okhalamo, amene anakhalitsa kuopsa kwao pa onse okhala momwemo! Pamenepo zisumbu zidzanjenjemera tsiku la kugwa kwako, inde zisumbu za kunyanja zidzatenga nkhawa pa kuchokera kwako. Pakuti atero Ambuye Yehova, Pamene ndikusandutsa mudzi wopasuka, ngati midzi yosakhalamo anthu, ndi kukukweretsera nyanja, nadzakumiza madzi aakulu; pamenepo ndidzakutsitsa nao otsikira kumanda, kwa anthu a kale lomwe, ndi kukukhalitsa kumalo a kunsi kwa dziko, kopasukira kale lomwe, pamodzi nao otsikira kumanda, kuti mwa iwe musakhale anthu; ndipo ndidzaika ulemerero m'dziko la amoyo, ndidzakuika woopsa; ndipo sudzaonekanso, chinkana akufunafuna sudzapezekanso konse, ati Ambuye Yehova. Anandidzeranso mau a Yehova, akuti, Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, Takwezera Tiro nyimbo ya maliro; nuti kwa Tiro, Iwe wakukhala polowera m'nyanja, wakuchita malonda ndi mitundu ya anthu m'zisumbu zambiri, atero Ambuye Yehova, Iwe, Tiro, wati, Ine ndine wokongola wangwiro. M'mphepete mwako muli m'kati mwa nyanja, iwo anakumanga iwe anakonza kukongola kwako kukhale kwangwiro. Anacheka matabwa ako onse amlombwa wa ku Seniri, anatenga mikungudza ya ku Lebanoni kukupangira milongoti. Anasema nkhafi zako za thundu wa ku Basani, anapanga mipando yako yamnyanga, woika mu mtengo wanaphini wochokera ku zisumbu za Kitimu. Thanga lako ndi labafuta wopikapika wa ku Ejipito, likhale ngati mbendera yako; chophimba chako ndicho nsalu yamadzi ndi yofiirira zochokera ku zisumbu za Elisa. Okhala m'Sidoni ndi Arivadi ndiwo opalasa ako; anzeru ako, Tiro, okhala mwa iwe, ndiwo oongolera ako. Akulu a ku Gebala ndi eni luso ake anali mwa iwe kukonza ziboo zako; zombo zonse za kunyanja pamodzi ndi amalinyero ao anali mwa iwe kusinthana nawe malonda. Apersiya, Aludi, Aputi, anali m'khamu lako; anthu ako a nkhondo anapachika chikopa ndi chisoti mwa iwe, anamveketsa kukoma kwako. Anthu a Arivadi pamodzi ndi ankhondo ako anali pa malinga ako pozungulira, ndi Agamadi anali mu nsanja zako; anapachika zikopa zao pa makoma ako pozungulira, anakwaniritsa kukoma kwako. Tarisisi anagulana nawe malonda m'kuchuluka kwa chuma chilichonse; anagula malonda ako ndi siliva ndi chitsulo, seta ndi ntovu. Yavani, Tubala, Meseki, anagulana nawe malonda; ndi anthu amoyo ndi zotengera zamkuwa anagulana nawe malonda. Iwo a nyumba ya Togarima anagula malonda ako ndi akavalo, ndi akavalo a nkhondo, ndi nyuru. Anthu a ku Dedani anakutsatsa malonda, zisumbu zambiri zinazolowerana nawe malonda ako, anabwera nazo minyanga ndi phingo kugulana nawe malonda. Aramu anachita nawe malonda chifukwa cha zambirizo udazipanga, anagula malonda ako ndi smaragido, nsalu yofiirira, ndi yopikapika, ndi bafuta, ndi korale, ndi ngale. Yuda ndi dziko la Israele anagulana nawe malonda, anagula malonda ako ndi tirigu wa ku Miniti, ndi zozuna, ndi uchi, ndi mafuta, ndi mafuta amankhwala. Damasiko anagulana nawe malonda chifukwa cha zambirizo udazipanga, chifukwa cha kuchuluka kwa chuma chilichonse, ndi vinyo wa ku Heliboni, ndi ubweya wa nkhosa woyera. Vedani ndi Yavani anagula malonda ako ndi thonje, unagulana nao chitsulo chosalala, ngaho, ndi nzimbe. Dedani anagulana nawe malonda ndi nsalu za mtengo wake zoyenda nazo pa kavalo. Arabiya ndi akalonga onse a ku Kedara anazolowerana nao malonda ako; anaankhosa, nkhosa zamphongo, ndi mbuzi, izi anagulana nawe. Amalonda a ku Sheba ndi a ku Raama anagulana nawe malonda; anagula malonda ako ndi zonunkhira zoposa zilizonse, ndi miyala iliyonse ya mtengo wake, ndi golide. Harani ndi Kane ndi Edeni, amalonda a ku Sheba Asiriya ndi Kilimadi, anagulana nawe malonda. Awa anagulana nawe malonda ndi zovala zosankhika, ndi mitumba ya nsalu zofiirira ndi zopikapika, ndi chuma cha thonje lopotapota, ndi zingwe zopota zolimba za malonda ako. Zombo za ku Tarisisi ndizo amtengatenga a malonda ako; ndipo unadzadzidwa ndi chuma ndi ulemu waukulu pakati pa nyanja. Opalasa ako anakufikitsa kumadzi aakulu; mphepo ya kum'mawa inakuthyola m'kati mwa nyanja. Chuma chako, zako zogulana nazo malonda ako, amalinyero ako, ndi oongolera ako, amisiri ako, ndi ogulitsa malonda ako, ndi ankhondo ako onse okhala mwa iwe, pamodzi ndi msonkhano wonse uli pakati pa iwe, adzagwa m'kati mwa nyanja tsiku la kugwa kwako. Pakumveka mfuu wa oongolera ako mabwalo ako adzagwedezeka. Ndi onse ogwira nkhafi, amalinyero, ndi oongolera onse a kunyanja, adzatsika kuzombo zao, nadzaima pamtunda, nadzamveketsa mau ao pa iwe, nadzalira mowawa mtima, nadzathira fumbi pamitu pao, nadzakunkhulira m'maphulusa, nadzameta mpala chifukwa cha iwe, nadzadzimangira ziguduli m'chuuno, nadzakulirira ndi mtima wowawa maliro owawa. Ndipo pakulira adzakukwezera nyimbo ya maliro, ndi kukulirira, ndi kuti, Wakunga Tiro ndani, wakunga uyu waonongeka pakati pa nyanja? Pakutuluka malonda ako m'nyanja unadzaza mitundu yambiri ya anthu, unalemeretsa mafumu a pa dziko lapansi ndi chuma chako chochuluka ndi malonda ako. Muja unathyoka ndi nyanja m'madzi akuya malonda ako ndi msonkhano wako wonse adagwa pakati pako. Onse okhala pa zisumbu adagwa nawe, ndi mafumu ao aopsedwa kwambiri, zikhululuka nkhope zao. Amalonda mwa mitundu ya anthu akunyodola, wakhala choopsetsa iwe, ndipo sudzakhalanso konse. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, uziti kwa kalonga wa Tiro, Atero Ambuye Yehova, Popeza mtima wako wadzikweza, nuti, Ine ndine Mulungu, ndikhala pa mpando wa Mulungu pakati pa nyanja, ungakhale uli munthu, wosati Mulungu, ungakhale waika mtima wako ngati mtima wa Mulungu, taona, ndiwe wanzeru woposa Daniele, palibe chinsinsi angakubisire; mwa nzeru zako ndi luntha lako wadzionerera chuma, wadzionereranso golide ndi siliva mwa chuma chako; mwa nzeru zako zazikulu ndi kugulana malonda kwako wachulukitsa chuma chako, ndi mtima wako wadzikuza chifukwa cha chuma chako; chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza waika mtima wako ngati mtima wa Mulungu; chifukwa chake taona ndidzakufikitsira alendo oopsa a mitundu ya anthu, iwo adzasololera malupanga ao nzeru zako zokongola, nadzaipsa kunyezimira kwako. Adzakutsitsira kumanda, nudzafa mafedwe a ophedwa m'kati mwa nyanja. Kodi udzanena ndithu pamaso pa iye wakupha iwe, Ine ndine Mulungu, pokhala uli munthu, wosati Mulungu, m'dzanja la iye wakupha iwe. Udzafa mafedwe a osadulidwa ndi dzanja la alendo, pakuti ndachinena, ati Ambuye Yehova. Nandidzeranso mau a Yehova, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, kweza nyimbo ya maliro yolirira mfumu ya Tiro, nuziti kwa iye, Atero Ambuye Yehova, Wakomera muyeso ndi chizindikiro, wodzala ndi nzeru wokongola wangwiro. Unali m'Edeni, munda wa Mulungu, mwala uliwonse wa mtengo wake unali chofunda chako, sardiyo, topazi, diamondi, berulo, sohamu, ndi yaspi, safiro, nofeki, bareketi, ndi golide; malingaka ako ndi akazi ako anakutumikira tsiku lolengedwa iwe zinakonzekeratu. Unali kerubi wodzozedwa wakuphimba, ndipo ndinakuika unali pa phiri lopatulika la Mulungu, anayendayenda pakati pa miyala yamoto. Unali wangwiro m'njira zako chilengedwere iwe, mpaka chinapezeka mwa iwe chosalungama. Mwa kuchuluka kwa malonda ako anakudzaza m'kati mwako ndi chiwawa, ndipo unachimwa; chifukwa chake ndinakukankha kukuchotsa pa phiri la Mulungu; ndipo ndinakuononga, kerubi wakuphimba iwe, kukuchotsa pakati pa miyala yamoto. Unadzikuza mtima chifukwa cha kukongola kwako, waipsa nzeru zako; chifukwa cha kuwala kwako ndakugwetsa pansi, ndakuika pamaso pa mafumu, kuti akupenye. Mwa mphulupulu zako zochuluka ndi malonda ako osalungama waipsa malo ako opatulika; chifukwa chake ndatulutsa moto m'kati mwako wakunyeketsa iwe; ndipo ndakusandutsa mapulusa panthaka pamaso pa onse akuona. Onse akudziwa iwe mwa mitundu ya anthu adzadabwa nawe; wasanduka choopsa, ndipo sudzakhalanso konse. Anandidzeranso mau a Yehova, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako ku Sidoni, nuunenere; uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona, nditsutsana nawe Sidoni, ndipo ndidzalemekezedwa pakati pako; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova pakuchita Ine maweruzo mwa uwu, ndi kuzindikiridwa Woyera mwa uwu. Pakuti ndidzatumiza mliri ndi mwazi ilowe m'makwalala ake, ndi olasidwa adzagwa m'kati mwake ndi lupanga lougwera pozungulira ponse; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Ndipo nyumba ya Israele siidzakhalanso nayo mitungwi yolasa, kapena minga yaululu ya aliyense wakuizinga ndi kuipeputsa; motero adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova. Atero Ambuye Yehova, Pakusonkhanitsa nyumba ya Israele mwa mitundu ya anthu anabalalikamo, ndidzazindikirika Woyera mwaiwowa, pamaso pa amitundu; ndipo adzakhala m'dziko mwaomwao ndinalipereka kwa Yakobo mtumiki wanga. Nadzakhalamo osatekeseka, nadzamanga nyumba, ndi kuoka mpesa m'mindamo, nadzakhalamo mosatekeseka, ndikatha kukwaniritsira maweruzo pa onse akuwapeputsa pozungulira pao; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao. Chaka chakhumi, mwezi wakhumi, tsiku lakhumi ndi chiwiri la mweziwo, anandidzera mau a Yehova, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako itsutsane naye Farao mfumu ya Aejipito, nunenere motsutsana ndi iye, ndi Ejipito lonse; nena, uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona nditsutsana nawe, Farao mfumu ya Aejipito, ng'ona yaikulu yakugona m'kati mwa mitsinje yake, imene ikuti, Mtsinje wanga ndi wangatu, ndadzipangira ndekha uwu. Koma ndidzaika mbedza m'kamwa mwako, ndi kumamatiritsa nsomba za m'mitsinje mwako kumamba ako; ndipo ndidzakukweza kukutulutsa m'kati mwa mitsinje yako, pamodzi ndi nsomba zonse za m'mitsinje mwako zomamatira pa mamba ako. Ndipo ndidzakutaya kuchipululu, iwe ndi nsomba zonse za m'mitsinje mwako; udzagwa kuthengo koyera, sudzaunjikidwa, kapena kuoledwa; ndakupereka ukhale chakudya cha zilombo za padziko, ndi mbalame za kumlengalenga. Ndi onse okhala m'Ejipito adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, popeza anakhalira nyumba ya Israele mchirikizo wabango. Muja anakugwira ndi dzanja unathyoka, ndi kulasa mapewa ao onse; ndi muja anakutsamira unathyoka, ndi kuwagwedeza ziuno zao zonse. Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona, ndikudzera ndi lupanga, ndi kukulikhira munthu ndi nyama. Ndi dziko la Ejipito lidzakhala lopasuka ndi labwinja; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, popeza anati, Mtsinjewo ndi wanga, ndinaulenga ndine. Chifukwa chake taona, nditsutsana ndi iwe ndi mitsinje yako, ndipo ndidzasandutsa dziko la Ejipito likhale lopasuka konse, ndi labwinja, kuyambira ku Migidoli mpaka ku nsanja ya Siyene kufikira malire a Kusi. Silidzapitamo phazi la munthu, kapena phazi la nyama losapitamo, losakhalamo anthu zaka makumi anai. Ndipo ndidzasandutsa dziko la Ejipito labwinja pakati pa maiko a mabwinja; ndi midzi yake pakati pa midzi yopasuka idzakhala yabwinja zaka makumi anai; ndipo ndidzamwaza Aejipito mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa m'maiko. Pakuti atero Ambuye Yehova, Zitatha zaka makumi anai ndidzasonkhanitsa Aejipito kumitundu ya anthu kumene anamwazikirako; ndipo ndidzabweza undende wa Ejipito, ndi kuwabwezera kudziko la Patirosi, kudziko la kubadwa kwao, ndi komweko adzakhala ufumu wopepuka. Udzakhala wopepuka wa maufumu onse, sudzadzikwezanso pa amitundu; ndipo ndidzawachepsa, kuti asachitenso ufumu pa amitundu. Ndipo sudzakhalanso chotama cha nyumba ya Israele, kukumbutsa mphulupulu, pakuwatembenukira kuwatsata; motero adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova. Ndipo kunali chaka cha makumi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri mwezi woyamba, tsiku loyamba la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anachititsa ankhondo ake ntchito yaikulu yoponyana ndi Tiro; mitu yonse inachita dazi, ndi mapewa onse ananyuka; koma analibe kulandira mphotho ya ku Tiro, iye kapena ankhondo ake, pa ntchito anagwirayo; chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona, ndidzapereka dziko la Ejipito kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni; ndipo adzachoka nao aunyinji ake, nadzafunkha ndi kulanda zake, ndizo mphotho ya khamu lake. Ndamninkha dziko la Ejipito chombwezera ntchito yake, popeza anandigwirira ntchito, ati Ambuye Yehova. Tsiku ilo ndidzameretsera nyumba ya Israele nyanga; ndipo ndidzakutsegulira pakamwa pakati pao; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Anandidzeranso mau a Yehova, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, nenera, uziti, Atero Ambuye Yehova, Liritsani, Ha, tsikulo! Pakuti layandikira tsiku, layandikira tsiku la Yehova, tsiku lamitambo, ndiyo nyengo ya amitundu. Ndi lupanga lidzadzera Ejipito, ndi m'Kusi mudzakhala kuwawa kwakukulu, pakugwa ophedwa m'Ejipito; ndipo adzachotsa aunyinji ake, ndi maziko ake adzagadamuka. Kusi, ndi Puti, ndi Ludi, ndi osokonezeka onse, ndi Libiya, ndi anthu a dziko lopangana nao, adzagwa pamodzi nao ndi lupanga. Atero Yehova, Iwonso ochirikiza Ejipito adzagwa, ndi mphamvu yake yodzikuza idzatsika, kuyambira ku Migidoli mpaka ku nsanja ya Siyene adzagwa m'kati mwake ndi lupanga, ati Ambuye Yehova. Ndipo adzakhala opasuka pakati pa maiko opasuka, ndi midzi yake idzakhala pakati pa midzi yopasuka. Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, nditaika moto m'Ejipito, naonongeka onse akumthandiza. Tsiku ilo mithenga idzatuluka pamaso panga m'zombo kuopsa Akusi osalabadira; ndipo kudzakhala kuwawa kwakukulu pakati pao, monga tsiku la Ejipito, pakuti taona, likudza. Atero Ambuye Yehova, Ndidzaleketsa kusokosera kwa Ejipito ndi dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni. Iye ndi anthu ake pamodzi naye, woopsa amitundu, adzatengedwa aliononge dzikolo, nadzasololera Ejipito malupanga ao, ndi kudzaza dziko ndi ophedwa. Ndipo ndidzaphwetsa mitsinje, ndi kugulira dziko m'dzanja la anthu oipa, ndipo ndidzalisandutsa likhale dziko lopasuka, ndi zonse zili m'mwemo mwa dzanja la alendo; Ine Yehova ndachinena. Atero Ambuye Yehova, Ndidzaononganso mafano, ndi kuleketsa milungu yopanda pake ku Nofu; ndipo sadzaonekanso kalonga wochokera ku Ejipito, ndipo ndidzaopsa dziko la Ejipito. Ndipo ndidzasandutsa Patirosi labwinja, ndi kuika moto m'Zowani, ndi kukwaniritsa maweruzo m'No. Ndipo ndidzatsanulira ukali wanga pa Sini, polimbika penipeni pa Ejipito, ndi kulikha aunyinji a No. Ndipo ndidzaika moto m'Ejipito; Sini adzamva kuwawa kwakukulu, ndi No adzagawika pakati, ndi Nofu adzaona adani usana. Anyamata a Oni ndi Pibeseti adzagwa ndi lupanga, ndi midziyi idzalowa undende. Ndi ku Tehafinehesi kudzada usana, pakuthyola Ine magoli a Ejipito komweko; ndi mphamvu yake yodzikuza idzalekeka m'menemo; kunena za ilo mtambo udzaliphimba, ndi ana ake akazi adzalowa undende. Motero ndidzakwaniritsa maweruzo m'Ejipito, ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Ndipo kunali chaka chakhumi ndi chimodzi, mwezi woyamba, tsiku lachisanu ndi chiwiri la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, ndathyola dzanja la Farao mfumu ya Aejipito, ndipo taona, silinamangidwa kuti lipole, kulikulunga ndi nsalu, kulilimbitsa ligwire lupanga. Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona, Ine ndilimbana naye Farao mfumu ya Aejipito, ndidzathyola manja ake, lolimba ndi lothyokalo, ndi kutayitsa lupanga m'dzanja lake. Ndipo ndidzamwaza Aejipito mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa m'maiko. Ndipo ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babiloni, ndi kuika lupanga langa m'dzanja lake; koma ndidzathyola manja a Farao, ndipo adzabuula pamaso pake mabuulo a munthu wopyozedwa. Ndipo ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babiloni, koma manja a Farao adzagwa; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova pakuika Ine lupanga langa m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni, nalitambasula iye pa dziko la Ejipito. Ndipo ndidzamwaza Aejipito mwa amitundu, ndi kuwabalalitsa mwa amitundu; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Ndipo kunali chaka chakhumi ndi chimodzi, mwezi wachitatu, tsiku loyamba la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, nena kwa Farao mfumu ya Aejipito ndi aunyinji ake, Ufanana ndi yani m'ukulu wako? Taona, Asiriya anali mkungudza wa ku Lebanoni ndi nthambi zokoma zovalira, wautali msinkhu, kunsonga kwake ndi kumitambo. Madzi anaumeretsa, chigumula chinaukulitsa, mitsinje yake inayenda, nizungulira munda wake, nipititsa michera yake kumitengo yonse ya kuthengoko. Chifukwa chake msinkhu wake unaposa mitengo yonse ya kuthengo, ndi nthambi zake zinachuluka, ndi nthawi zake zinatalika, chifukwa cha madzi ambiri pophuka uwu. Mbalame zonse za m'mlengalenga zinamanga zisa zao pa nthambi zake, ndi pansi pa nthawi zake zinaswana nyama zonse za kuthengo, ndi pa mthunzi wake inakhala mitundu yonse yaikulu ya anthu. M'mwemo unakoma m'ukulu wake, m'kutalika kwa nthawi zake, popeza muzu wake unakhala kumadzi ambiri. Mikungudza ya m'munda wa Mulungu siinathe kuubisa, milombwa siinanga nthambi zake, mifula siinanga nthawi zake; m'munda wa Mulungu munalibe mtengo wofanana nao kukoma kwake. Ndinaupanga wokoma ndi nthawi zake zochuluka; ndi mitengo yonse ya m'Edeni inali m'munda wa Mulungu inachita nao nsanje. Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza mtengowo unakuza msinkhu wake, nufikitsa nsonga yake kumitambo, nukwezeka mtima wake m'kukula kwake, ndidzaupereka m'dzanja la wamphamvu wa amitundu; iye adzachita naotu, Ine ndautaya mwa choipa chake. Ndipo alendo oopsawo a amitundu anaulikhatu, nausiya; nthawi zake zidagwa pamapiri ndi m'zigwa zonse, ndi nthambi zake zinathyokera ku timitsinje tonse ta m'dziko; ndi mitundu yonse ya anthu a pa dziko lapansi inatsika kumthunzi wake, niusiya. Pogwera pake padzakhala mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi nyama zonse za kuthengo zidzakhala pa nthambi zake; kuti mitengo iliyonse ya kumadzi isadzikuze chifukwa cha msinkhu wao, kapena kufikitsa nsonga zao pakati pa mitambo, ndi kuti amphamvu ao asaime m'kukula kwao, ndiwo onse akumwa madzi; pakuti onsewo aperekedwa kuimfa munsi mwake mwa dziko, pakati pa ana a anthu, pamodzi ndi iwo otsikira kumanda. Atero Ambuye Yehova, Tsiku lija anatsikira kumanda ndinachititsa maliro, ndinamphimbira nyanja, ndinachepsa mitsinje yake, ndi madzi aakulu analetseka; ndipo ndinamdetsera Lebanoni, ndi mitengo yonse ya kuthengo inafota chifukwa cha uwo. Ndinagwedeza amitundu ndi phokoso la kugwa kwake, muja ndinagwetsera kumanda, pamodzi ndi iwo otsikira kumanda; ndi mitengo yonse ya ku Edeni yosankhika, ndi yokometsetsa ya ku Lebanoni, yonse yakumwa madzi, inasangalala munsi mwake mwa dziko lapansi. Iwonso anatsika naye kumanda kwa iwo ophedwa ndi lupanga, ndiwo amene adakhala dzanja lake okhala mumthunzi mwake pakati pa amitundu. Momwemo ufanana ndi yani m'ulemerero ndi ukulu pakati pa mitengo ya Edeni? Koma udzatsitsidwa pamodzi ndi mitengo ya Edeni munsi mwake mwa dziko lapansi, udzagona pakati pa osadulidwa, pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga. Uwu ndi Farao ndi aunyinji ake onse, ati Ambuye Yehova. Ndipo kunali chaka chakhumi ndi chiwiri, mwezi wakhumi ndi chiwiri, tsiku loyamba la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, takwezera Farao mfumu ya Aejipito nyimbo yamaliro; uziti naye, Unafanana nao msona wa mkango wa amitundu, unanga ng'ona ya m'nyanja, unabuka m'mitsinje mwako, nuvundulira madzi ndi mapazi ako, ndi kudetsa mitsinje yao. Atero Ambuye Yehova, Ndidzakuponyera khoka langa mwa msonkhano wa mitundu yambiri ya anthu, nadzakuvuulira m'khoka mwanga. Ndipo ndidzakusiya pamtunda, ndidzakuponya kuthengo koyera, ndi kuteretsa pa iwe mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi kukhutitsa zilombo za dziko lonse lapansi ndi iwe. Ndipo ndidzaika nyama yako pamapiri, ndi kudzaza zigwa ndi msinkhu wako. Ndipo ndidzamwetsa dziko losambiramo iwe ndi mwazi wako, kufikira kumapiri; ndi mitsinje idzadzala nawe. Ndipo pakukuzima iwe ndidzaphimba thambo, ndi kudetsa nyenyezi zake; ndidzaphimba dzuwa ndi mtambo, ndi mwezi sudzaonetsa kuwala kwake. Ndidzakudetsera miyuni yonse yakuunikira kuthambo, ndi kuchititsa mdima pa dziko lako, ati Ambuye Yehova. Ndidzavutanso mitima ya mitundu yambiri ya anthu, pakufikitsa Ine chionongeko chako mwa amitundu, m'maiko amene sunawadziwa. Ndipo ndidzasumwitsa nawe mitundu yambiri ya anthu, ndi mafumu ao adzachita malunga chifukwa cha iwe, pakung'animitsa Ine lupanga langa pamaso pao; ndipo adzanjenjemera mphindi zonse, yense chifukwa cha moyo wake tsiku lakugwa iwe. Pakuti atero Ambuye Yehova, Lupanga la mfumu ya ku Babiloni lidzakudzera. Ndidzagwetsa aunyinji ako ndi malupanga a eni mphamvu, ndiwo onse oopsetsa a amitundu; ndipo adzaipsa kudzikuza kwa Ejipito, ndi aunyinji ake onse adzaonongeka. Ndidzaononganso nyama zake zonse za kumadzi ambiri; ndi phazi la munthu silidzavundulira, ndi ziboda za nyama zosawavundulira. Pamenepo ndidzadikhitsa madzi ake, ndi kuyendetsa madzi a m'mitsinje mwao ngati mafuta, ati Ambuye Yehova. Pakusanduliza Ine dziko la Ejipito likhale lopasuka ndi labwinja, dziko losowa zodzaza zake, pakukantha Ine onse okhala m'mwemo, pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Iyi ndi nyimbo ya maliro adzalira nayo, ana akazi a amitundu adzachita nayo maliro; adzalirira nayo Ejipito ndi aunyinji ake onse, ati Ambuye Yehova. Kunalinso chaka chakhumi ndi chiwiri, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi, anandidzera mau a Yehova, ndi kuti, Wobadwa ndi munthu iwe, lirira aunyinji a Ejipito, nuwagwetsere iye ndi ana akazi a amitundu omveka kunsi kwa dziko, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje. Uposa yani m'kukoma kwako? Tsika, nuikidwe ndi osadulidwa. Adzagwa pakati pa iwo ophedwa ndi lupanga, operekedwa kwa lupanga, mkokereko ndi aunyinji ake onse. Amphamvu oposa ali m'kati mwa manda adzanena naye, pamodzi ndi othandiza ake, Anatsikira, agonako osadulidwawo, ophedwa ndi lupanga. Asiriya ali komwe ndi msonkhano wake wonse, manda ake amzinga; ophedwa onsewo, adagwa ndi lupanga; manda ao aikidwa ku malekezero a dzenje, ndi gulu lake lizinga manda ake; ophedwa onsewo adagwa ndi lupanga, amene anopsetsa m'dziko la amoyo. Elamu ali komwe ndi gulu lake lonse lozinga manda ake; ophedwa onsewo, adagwa ndi lupanga; amene anatsikira osadulidwa kunsi kwake kwa dziko, amene anaopsetsa m'dziko la amoyo, nasenza manyazi ao, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje. Pakati pa ophedwa anamuikira kama, iye ndi aunyinji ake onse, manda ake amzinga, onsewo osadulidwa, ophedwa ndi lupanga, pakuti anaopsetsa la amoyo, nasenza manyazi ao, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje, aikidwa pakati pa ophedwa. Meseki, Tubala, ndi aunyinji ake onse ali komweko, manda ake amzinga; onsewo osadulidwa, ophedwa ndi lupanga; pakuti anaopsetsa m'dziko la amoyo. Koma sagona pamodzi ndi amphamvu osadulidwa adagwawo amene anatsikira kumanda ndi zida zao za nkhondo, amene anawatsamiritsa malupanga ao; ndi mphulupulu zao zili pa mafupa ao; pakuti anaopsetsa amphamvu m'dziko la amoyo. Ndipo udzathyoledwa pakati pa osadulidwa, nudzagona pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga. Edomu ali komwe, mafumu ake ndi akalonga ake onse, amene anaikidwa mu mphamvu yao, pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga; agona pamodzi ndi osadulidwa, ndi iwo akutsikira kudzenje. Akalonga a kumpoto ali komwe onsewo, ndi Asidoni onse, amene anatsikira pamodzi ndi ophedwa, nachita manyazi chifukwa cha kuopsetsa anachititsaku ndi mphamvu yao, nagona osadulidwa pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga, nasenza manyazi ao pamodzi ndi iwo otsikira kudzenje. Farao adzawaona, nadzasangalala nao aunyinji ake onse, Farao ndi ankhondo ake onse ophedwa ndi lupanga, ati Ambuye Yehova. Pakuti ndinaika kuopsa kwake m'dziko la amoyo; ndipo adzaikidwa pakati pa osadulidwa, pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga, ndiye Farao ndi aunyinji ake onse, ati Ambuye Yehova. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, Nena ndi ana a anthu a mtundu wako, uziti nao, Ndikafikitsira dziko lililonse lupanga, nakatenga eni dziko munthu wa pakati pao, nakamuika awadikirire, nakaona iye lupanga lilikudzera dziko, nakaomba lipenga ndi kuchenjeza anthu; ndipo wina, kumva adamva mau a lipenga, koma osalabadira, likadza lupanga, nilimchotsa, wadziphetsa ndi mtima wake. Anamva mau a lipenga, osawalabadira, wadziphetsa ndi mtima wake; akadalabadira, akadalanditsa moyo wake. Koma mlonda akaona lupanga likudza, osaomba lipenga, osachenjeza anthu, nilidza lupanga, nilichotsa mwa iwo; munthu atengedwadi m'mphulupulu zake, koma mwazi wake ndidzaufunsa pa dzanja la mlonda. Iwe tsono, wobadwa ndi munthu, ndakuika mlonda wa nyumba ya Israele, m'mwemo imva mau a pakamwa panga, nundichenjezere iwo. Ndikati Ine kwa woipa, Woipawe, udzafa ndithu, osanena iwe kumchenjeza woipayo aleke njira yake, woipa uyo adzafa m'mphulupulu yake, koma mwazi wake ndidzaufunsa pa dzanja lako. Koma ukachenjeza woipa za njira yake, aileke; koma iye osaileka njira yake, adzafa m'mphulupulu mwake iye, koma iwe walanditsa moyo wako. Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, nena kwa nyumba ya Israele, Mumatero inu ndi kuti, Zolakwa zathu ndi zochimwa zathu zitikhalira, ndipo tichita nazo liwondewonde, tidzakhala ndi moyo bwanji? Uziti nao, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindikondwera nayo imfa ya woipa, koma kuti woipa aleke njira yake, nakhale ndi moyo; bwererani, bwererani, kuleka njira zanu zoipa, muferenji inu nyumba ya Israele? Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, unene ndi ana a anthu a mtundu wako, Cholungama cha wolungama sichidzamlanditsa tsiku la kulakwa kwake, ndi kunena za choipa cha woipa, sadzagwa nacho tsiku lakubwerera iye kuleka choipa chake; ndi munthu wolungama sadzakhoza kukhala ndi moyo ndi chilungamo chake tsiku lakuchimwa iye. Ndikanena kwa wolungama kuti adzakhala ndi moyo ndithu, akatama chilungamo chake, akachita chosalungama, sizikumbukika zolungama zake zilizonse; koma m'chosalungama chake anachichita momwemo adzafa. Ndipo ndikanena kwa woipa, Udzafa ndithu: koma akabwerera iye kuleka tchimo lake, nakachita choyenera ndi cholungama; woipayo akabweza chikole, nakabweza icho anachilanda mwachifwamba, nakayenda m'malemba a moyo wosachita chosalungama, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa. Zoipa zake zilizonse anazichita sizidzakumbukika zimtsutse, anachita choyenera ndi cholungama, adzakhala ndi moyo ndithu. Koma ana a anthu a mtundu wako akuti, Njira ya Ambuye siiyenera; koma iwowa njira yao siiyenera. Akabwerera wolungama kuleka chilungamo chake, nakachita chosalungama, adzafa m'mwemo. Ndipo woipa akabwerera kuleka choipa chake, nakachita choyenera ndi cholungama, adzakhala ndi moyo nazo. Koma munati, Njira ya Ambuye siiyenera. Nyumba ya Israele inu, ndidzakuweruzani, yense monga mwa njira zake. Ndipo kunali chaka chakhumi ndi chiwiri cha undende wathu, mwezi wakhumi, tsiku lachisanu la mweziwo, anandidzera wina wopulumuka ku Yerusalemu, ndi kuti, Wakanthidwa mudzi. Koma dzanja la Yehova linandikhalira madzulo, asanandifike wopulumukayo; ndipo ananditsegula pakamwa mpaka anandifika m'mawa, m'mwemo panatseguka pakamwa panga, wosakhalanso wosalankhula. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, iwo okhala kumabwinja a dziko la Israele anena, ndi kuti, Abrahamu anali yekha, nakhala nalo dziko cholowa chake; koma ife ndife ambiri, dzikoli lipatsidwa kwa ife cholowa chathu. Chifukwa chake unene nao, Atero Ambuye Yehova, Mumadyera kumodzi ndi mwazi, mumakwezera maso anu kumafano anu, ndi kukhetsa mwazi; ndipo kodi mudzakhala nalo dziko cholowa chanu? Mumatama lupanga lanu, mumachita chonyansa, mumaipsa yense mkazi wa mnansi wake; ndipo kodi mudzakhala nalo dziko cholowa chanu? Uzitero nao, Atero Ambuye Yehova, Pali Ine, iwo okhala kumabwinja adzagwadi ndi lupanga, ndi iye ali kuthengo koyera ndidzampereka kwa zilombo, adyedwe nazo; ndi iwo okhala m'malinga ndi m'mapanga adzafa ndi mliri. Ndipo ndidzasanduliza dziko likhale lachipululu ndi lodabwitsa, ndi mphamvu yake yodzikuza idzatha, ndi mapiri a Israele adzakhala achipululu, osapitako munthu. Pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, posanduliza Ine dziko likhale lachipululu ndi lodabwitsa, chifukwa cha zonyansa zao zonse anazichita. Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, ana a anthu a mtundu wako anena za iwe kumakoma ndi kumakomo a nyumba zao, nanenana yense ndi mbale wake, ndi kuti, Tiyeni tikamve mau ofuma kwa Yehova. Ndipo akudzera monga amadzera anthu, nakhala pansi pamaso pako ngati anthu anga, namva mau ako, koma osawachita; pakuti pakamwa pao anena mwachikondi, koma mtima wao utsata phindu lao. Ndipo taona, akuyesa iwe ngati nyimbo yachikondi ya woimba bwino, woimba limba bwino; pakuti akumva mau ako, koma osawachita. Ndipo pakuchitika ichi, pakuti chifikadi, pamenepo adzadziwa kuti panali mneneri pakati pao. Ndipo mau a Yehova anandidzera, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, Nenera motsutsa abusa a Israele; nenera, nuti nao abusawo, Atero Ambuye Yehova, Tsoka abusa a Israele odzidyetsa okha; kodi abusa sayenera kudyetsa nkhosa? Mukudya mafuta, muvala ubweya, mukupha zonenepa; koma simudyetsa nkhosa. Zofooka simunazilimbitsa; yodwala simunaichiritsa, yothyoka simunailukira chika, yopirikitsidwa simunaibweza, yotayika simunaifuna; koma munazilamulira mwamphamvu ndi moopsa. M'mwemo zinamwazika posowa mbusa, nizinakhala chakudya cha zilombo zilizonse za kuthengo, popeza zinamwazika. Nkhosa zanga zinasokera kumapiri ali onse, ndi pa chitunda chilichonse chachitali; inde nkhosa zanga zinabalalika pa dziko lonse lapansi, ndipo panalibe wakuzipwaira kapena kuzifunafuna. Chifukwa chake abusa inu, imvani mau a Yehova: Pali Ine, ati Ambuye Yehova, zedi, popeza nkhosa zanga zinakhala nyama, ndi nkhosa zanga zinakhala chakudya cha zilombo zonse za kuthengo, chifukwa kunalibe mbusa, ndi abusa anga sanafunafune nkhosa zanga, koma abusawo anadzidyetsa okha, osadyetsa nkhosa zanga; chifukwa chake, abusa inu, imvani mau a Yehova: Atero Ambuye Yehova, Taonani, Ine ndiipidwa nao abusa, ndidzafunsa nkhosa zanga pa dzanja lao, ndi kuwaletsa asadyetsenso nkhosazo, ngakhale kudzidyetsa okha sadzachitanso; ndipo ndidzalanditsa nkhosa zanga pakamwa pao, zisakhale chakudya chao. Pakuti atero Ambuye Yehova, Taonani, Ine, Inedi ndidzapwaira nkhosa zanga ndi kuzifunafuna. Monga mbusa afunafuna nkhosa zake tsiku lokhala iye pakati pa nkhosa zake zobalalika, momwemo ndidzafunafuna nkhosa zanga; ndipo ndidzawalanditsa m'malo monse anabalalikamo tsiku la mitambo ndi la mdima. Ndipo ndidzazitulutsa mwa mitundu ya anthu, ndi kuzisonkhanitsa m'maiko, ndi kulowa nazo m'dziko lao; ndipo ndidzazidyetsa pa mapiri a Israele, patimitsinje, ndi ponse pokhala anthu m'dziko. Ndidzazidyetsa podyetsa pabwino; ndi pa mapiri atali a Israele padzakhala kholo lao, apo adzagona m'khola mwabwino, nadzadya podyetsa pokometsera pa mapiri a Israele. Ine ndekha ndidzadyetsa nkhosa zanga, ndi kuzigonetsa, ati Ambuye Yehova. Ndidzafuna yotayika, ndi kubweza yopirikitsidwa, ndi kulukira chika yothyoka mwendo, ndikulimbitsa yodwalayo; koma yonenepa ndi yolimba ndidzaziononga, ndidzazidyetsa ndi chiweruzo. Ndipo inu, gulu langa, atero Ambuye Yehova, ndiweruza pakati pa zoweta ndi zoweta, nkhosa zamphongo ndi atonde. Kodi chikucheperani, kuti mwadya podyetsa pabwino? Muyenera kodi kupondereza ndi mapazi anu podyera panu potsala? Muyenera kumwa madzi odikha, ndi kuvundulira otsalawo ndi mapazi anu? Ndi nkhosa zanga zidye kodi zoponderezeka ndi mapazi anu, ndi kumwa zovunduliridwa ndi mapazi anu? Chifukwa chake atero nao Ambuye Yehova, Taonani, Ine, Inedi ndidzaweruza pakati pa zoweta zonenepa, ndi zoweta zoonda. Popeza mukankha ndi nthiti ndi phewa, nimugunda zodwala zonse ndi nyanga zanu, mpaka mwazibalalitsa kubwalo, chifukwa chake ndidzapulumutsa gulu langa lisakhalenso chakudya; ndipo ndidzaweruza pakati pa zoweta ndi zoweta. Ndipo ndidzaziutsira mbusa mmodzi; iye adzazidyetsa, ndiye mtumiki wanga Davide, iye adzazidyetsa, nadzakhala mbusa wao. Ndipo Ine Yehova ndidzakhala Mulungu wao, ndi mtumiki wanga Davide kalonga pakati pao; Ine Yehova ndanena. Ndipo ndidzapangana nazo pangano la mtendere, ndi kuleketsa zilombo zoipa m'dzikomo; ndipo zidzakhala mosatekeseka m'chipululu, ndi kugona kunkhalango. Pakuti ndidzaika izi ndi milaga yozungulira chitunda changa, zikhale mdalitso; ndipo ndidzavumbitsa mivumbi m'nyengo yake, padzakhala mivumbi ya madalitso. Ndi mitengo ya kuthengo idzapereka zobala zao, ndi nthaka idzapereka zipatso zake, ndipo adzakhazikika m'dziko mwao; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, nditadula zomangira goli lao, ndi kuwalanditsa m'manja mwa iwo akuwatumikiritsa. Ndipo sadzakhalanso chakudya cha amitundu, ndi chilombo cha kuthengo sichidzawadyanso; koma adzakhala osatekeseka, opanda wina wakuwaopsa. Ndipo ndidzawautsira mbeu yomveka, ndipo sadzachotsedwanso ndi njala m'dzikomo, kapena kusenzanso manyazi a amitundu. Ndipo adzadziwa kuti Ine Yehova Mulungu wao ndili nao, ndi kuti iwo, nyumba ya Israele, ndiwo anthu anga, ati Ambuye Yehova. Ndipo inu nkhosa zanga, nkhosa zapabusa panga, ndinu anthu, ndi Ine ndine Mulungu wanu, ati Ambuye Yehova. Nandidzeranso mau a Yehova, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, Lozetsa nkhope yako kuphiri la Seiri, nulinenere molitsutsa; nuti nalo, Atero Ambuye Yehova, Taona, ndiipidwa nawe phiri la Seiri, ndipo ndidzakutambasulira dzanja langa, ndi kukusanduliza lachipululu ndi lodabwitsa. Ndidzapasula midzi yako, nudzakhala lachipululu; ndipo udzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Popeza uli nao udani wosatha, waperekanso ana a Israele kumphamvu ya lupanga m'nthawi ya tsoka lao, mu nthawi ya mphulupulu yotsiriza; chifukwa chake, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, ndikukonzeratu uphedwe, ndi mwazi udzakulondola; popeza sunadana nao mwazi, mwazi udzakulondola. Ndipo ndidzaika phiri la Seiri lodabwitsa ndi lachipululu, ndi kuononga pomwepo wopitapo ndi wobwerapo. Ndipo ndidzadzaza mapiri ake ndi ophedwa ake pa zitunda zako, ndi m'zigwa zako, ndi m'mitsinje mwako monse; adzagwa ophedwa ndi lupanga. Ndidzakusandutsa mabwinja osatha; ndi m'midzi mwako simudzakhalanso anthu; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Popeza wanena, Mitundu iwiri iyi ya anthu ndi maiko awiri awa adzakhala anga, tidzakhala nao ngati cholowa chathu, angakhale Yehova anali komweko; chifukwa chake, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, ndidzachita monga mwa mkwiyo wako, ndi monga mwa nsanje yako unachita nayo pa kukwiya nao iwe; ndipo ndidzadziwika nao pamene ndikuweruza. Ndipo udzadziwa kuti Ine Yehova ndidamva zamwano zako zonse udazinena pa mapiri a Israele, ndi kuti, Apasuka, apatsidwa kwa ife tiwadye. Ndipo pakamwa panu mwadzikuza pa Ine, ndi kundichulukitsira mau anu ndawamva Ine. Atero Ambuye Yehova, Pokondwerera dziko lonse ndidzakusanduliza lachipululu. Monga momwe unakondwerera cholowa cha nyumba ya Israele, popeza chidapasuka, momwemo ndidzakuchitira iwe; udzakhala wopasuka, phiri la Seiri iwe, ndi Edomu lonse lonseli; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu, unenere kwa mapiri a Israele, uziti, Mapiri a Israele inu, imvani mau a Yehova. Atero Ambuye Yehova, Popeza mdani ananena za inu, Onyo, ingakhale misanje yakale ili yathu, cholowa chathu; chifukwa chake unenere, nuti, Atero Ambuye Yehova, Chifukwa, inde chifukwa kuti anakupasulani, nakumemezani pozungulira ponse, kuti mukhale cholowa cha amitundu otsala, ndipo mwafika pa milomo ya akazitape, ndi pa mbiri yoipa ya anthu; chifukwa chake, mapiri inu a Israele, imvani mau a Ambuye Yehova. Atero Ambuye Yehova kunena ndi mapiri, ndi zitunda, ndi mitsinje, ndi zigwa, ndi zipululu zopasuka, ndi midzi yamabwinja, imene yakhala chakudya ndi choseketsa amitundu otsala akuzungulira; chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Zoonadi pa nsanje yanga yodya nayo moto ndinanena motsutsana nao amitundu otsala, ndi Edomu lonse, amene anadzipatsira dziko langa likhale cholowa chao ndi chimwemwe cha mtima wonse, ndi mtima wopeputsa, kuti alande zake zonse zikhale zofunkha. Chifukwa chake unenere za dziko la Israele, nuti kwa mapiri ndi kwa zitunda, kwa mitsinje ndi kwa zigwa, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndalankhula mu nsanje yanga ndi ukali wanga, popeza mwasenza manyazi a amitundu; chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Ndakweza dzanja langa Ine, ndi kuti, Zedi amitundu akuzungulira inu adzasenza manyazi ao. Koma inu, mapiri a Israele, mudzaphukitsa nthambi zanu, ndi kubalira anthu anga Israele zipatso zanu, pakuti ayandikira kufika. Pakuti taonani, Ine ndikhalira nanu kumodzi, ndipo ndidzakutembenukirani; ndipo mudzabzalidwa ndi kupaliridwa, ndipo ndidzakuchulukitsani anthu nyumba yonse ya Israele, yonseyi, ndi m'midzimo mudzakhala anthu, ndi kumabwinja kudzamangidwa midzi. Ndipo ndidzakuchulukitsirani anthu ndi nyama; ndipo adzachuluka, nadzabalana; ndipo ndidzakhalitsa anthu pa inu, monga umo anakhalira kale, ndipo ndidzachitira inu zabwino koposa poyamba paja; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Ndipo ndidzayendetsa anthu pa inu, ndiwo anthu anga Israele; adzakhala nawe dziko laolao, ndipo udzakhala cholowa chao osafetsanso ana ao. Atero Ambuye Yehova, Popeza akuti nawe, Dzikowe ukudya anthu, nuyesa anthu ako afedwa; chifukwa chake sudzadyanso anthu, kapena kuyesanso a mtundu wako afedwa, ati Ambuye Yehova. Ndipo sindidzakumvetsanso za manyazi a amitundu, ndipo sudzasenzanso mtonzo wa mitundu ya anthu, kapena kukhumudwitsanso anthu ako, ati Ambuye Yehova. Mau a Yehova anandidzeranso, ndi kuti, Wobadwa ndi munthu iwe, muja a nyumba ya Israele anakhala m'dziko mwao, analidetsa ndi njira yao, ndi machitidwe ao; njira yao pamaso panga inanga chidetso cha mkazi wooloka. M'mwemo ndinawatsanulira ukali wanga, chifukwa cha mwazi anautsanulira padziko, ndi chifukwa cha mafano analidetsa dziko nao; ndipo ndinawabalalitsa mwa amitundu, namwazika m'maiko monga mwa njira yao; ndi monga mwa machitidwe ao ndinawaweruza. Ndipo pofika iwo kwa amitundu kumene anamukako, anadetsa dzina langa loyera; popeza anthu ananena za iwowa, Awa ndi anthu a Yehova, natuluka m'dziko mwake. Koma ndinawaleka chifukwa cha dzina langa loyera, limene a nyumba ya Israele adalidetsa pakati pa amitundu, kumene adamkako. Chifukwa chake nena kwa nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Sindichichita ichi chifukwa cha inu, nyumba ya Israele, koma chifukwa cha dzina langa loyera munaliipsalo pakati pa amitundu, kumene mudamukako. Ndipo ndidzazindikiritsa dzina langa lalikulu kuti lili loyera, limene laipitsidwa mwa amitundu, limene inu munaliipsa pakati pao; ndipo amitundu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ati Ambuye Yehova, pozindikiridwa Ine woyera mwa inu pamaso pao. Pakuti ndidzakutengani kukutulutsani kwa amitundu, ndi kukusokolotsani m'maiko onse, ndi kubwera nanu m'dziko lanu. Ndipo ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera; ndidzakuyeretsani kukuchotserani zodetsa zanu zonse, ndi mafano anu nonse. Ndipo ndidzakupatsani mtima watsopano, ndi kulonga m'kati mwanu mzimu watsopano; ndipo ndidzachotsa mtima wamwala m'thupi, ndi kukupatsani mtima wamnofu. Ndipo ndidzaika mzimu wanga m'kati mwanu, ndi kukuyendetsani m'malemba anga; ndipo mudzasunga maweruzo anga ndi kuwachita. Ndipo mudzakhala m'dziko ndinapatsa makolo anulo, ndipo mudzakhala anthu anga, ndi Ine ndidzakhala Mulungu wanu. Ndipo ndidzakupulumutsani kwa zodetsa zanu zonse, ndidzaitananso tirigu ndi kumchulukitsa, osaikiranso inu njala. Ndipo ndidzachulukitsa zobala za mitengo, ndi zipatso za m'munda, kuti musalandirenso chitonzo cha njala mwa amitundu. Pamenepo mudzakumbukira njira zanu zoipa, ndi zochita inu zimene sizinali zabwino; ndipo mudzanyansidwa nokha pamaso panu, chifukwa cha mphulupulu zanu ndi zonyansa zanu. Dziwani kuti sindichita ichi chifukwa cha inu, ati Ambuye Yehova; chitani manyazi, dodomani, chifukwa cha njira zanu, nyumba ya Israele inu. Atero Ambuye Yehova, Tsiku loti ndikuyeretsani kukuchotserani mphulupulu zanu zonse, ndidzakhalitsa anthu m'midzimo; ndi pamabwinja padzamangidwa. Ndi dziko lachipululu lidzalimidwa, chinkana linali lachipululu pamaso pa onse opitako. Ndipo adzati, Dziko ili lachipululu lasanduka ngati munda wa Edeni ndi midzi yamabwinja, ndi yachipululu, ndi yopasuka, yamangidwa malinga, muli anthu m'mwemo. Pamenepo amitundu otsala pozungulira panu adzadziwa kuti Ine Yehova ndamanga malo opasuka, ndi kubzala pamene panali chipululu; Ine Yehova ndanena ndidzachita. Atero Ambuye Yehova, Ichi chomwe adzandipempha a nyumba ya Israele ndiwachitire ichi, ndidzawachulukitsira anthu ngati nkhosa. Ngati nkhosa za nsembe, ngati nkhosa za ku Yerusalemu pa zikondwerero zake zoikika, momwemo midzi yamabwinja idzadzala nao magulu a anthu; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Dzanja la Yehova linandikhalira, ndipo anatuluka nane mu mzimu wa Yehova, nandiika m'kati mwa chigwa, ndicho chodzala ndi mafupa; ndipo anandipititsa pamenepo pozungulira ponse, ndipo taonani, anali aunyinji pachigwa pansi, ndipo anaumitsitsa. Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, mafupa awa nkukhala ndi moyo kodi? Ndipo ndinati, Ambuye Yehova, mudziwa ndinu. Pamenepo anati kwa ine, Nenera kwa mafupa awa, nuti nao, Mafupa ouma inu, imvani mau a Yehova. Atero Ambuye Yehova kwa mafupa awa, Taonani, ndidzalonga mpweya mwa inu, ndipo mudzakhala ndi moyo. Ndipo ndidzakuikirani mtsempha, ndi kufikitsira inu mnofu, ndi kukuta inu ndi khungu, ndi kulonga mpweya mwa inu; ndipo mudzakhala ndi moyo; motero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. M'mwemo ndinanenera monga anandiuza, ndipo ponenera ine panali phokoso; ndipo taonani, panali gobedegobede, ndi mafupa anasendererana, fupa kutsata fupa linzake. Ndipo ndinapenya, taonani, panali mitsempha pa iwo, panadzaponso mnofu, ndi khungu linawakuta pamwamba pake; koma munalibe mpweya mwa iwo. Ndipo anati kwa ine, Nenera kwa mpweya, nenera, wobadwa ndi munthu iwe, nuti kwa mpweya, Atero Ambuye Yehova, Idza, mpweya iwe, kuchokera kumphepo zinai, nuuzire ophedwa awa, kuti akhale ndi moyo. M'mwemo ndinanenera monga anandiuza, ndi mpweya unawalowa, ndipo anakhala ndi moyo, naimirira chilili, gulu la nkhondo lalikulukulu ndithu. Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, Mafupa awa ndiwo nyumba yonse ya Israele; taonani, akuti, Mafupa athu auma, chiyembekezo chathu chatayika, talikhidwa. Chifukwa chake, nenera, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani anthu anga, ndidzatsegula kumanda kwanu, ndi kukweza inu mutuluke m'manda mwanu, ndipo ndidzakulowetsani m'dziko la Israele. Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova potsegula Ine kumanda kwanu, ndi kukweza inu kukutulutsani m'manda mwanu, anthu anga inu. Ndipo ndidzalonga mzimu wanga mwa inu, nimudzakhala ndi moyo; ndipo ndidzakukhazikani m'dziko mwanu; motero mudzadziwa kuti Ine Yehova ndanena ndi kuchichita, ati Yehova. Anandidzeranso mau a Yehova, akuti, Tsono, iwe wobadwa ndi munthu, Tenga mtengo umodzi, nulembepo, Wa Yuda ndi wa ana a Israele anzake; nutenge mtengo wina, nulembepo, Wa Yosefe, mtengo wa Efuremu, ndi wa nyumba yonse ya Israele anzake; nuiphatikize wina ndi unzake ikhale mtengo umodzi m'dzanja lako. Ndipo ana a anthu a mtundu wako akanena ndi iwe, ndi kuti, Sutifotokozera nanga zitani izi? Unene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndidzatenga mtengo wa Yosefe uli m'dzanja la Efuremu, ndi wa mafuko a Israele anzake, ndi kuwaika pamodzi ndi mtengo wa Yuda, ndi kuiyesa mtengo umodzi; ndipo idzakhala umodzi m'dzanja langa. Ndipo mitengo imene ulembapo idzakhala m'dzanja mwako pamaso pao. Nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndidzatenga ana a Israele pakati pa amitundu kumene adamkako, ndi kuwasokolotsa kumbali zonse, ndi kulowa nao m'dziko mwao; ndipo ndidzawayesa mtundu umodzi m'dzikomo, pa mapiri a Israele; ndipo mfumu imodzi idzakhala mfumu ya iwo onse, sadzakhalanso mitundu iwiri, kapena kugawanikanso maufumu awiri konse ai. Ndipo sadzadzidetsanso ndi mafano ao, kapena ndi zonyansa zao, kapena ndi zolakwa zao zilizonse; koma ndidzawapulumutsa mokhala mwao monse m'mene anachimwamo, ndi kuwayeretsa; m'mwemo adzakhala anthu anga, ndi Ine ndidzakhala Mulungu wao. Ndi mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu yao, ndipo iwo onse adzakhala ndi mbusa mmodzi, adzayendanso m'maweruzo anga, nadzasunga malemba anga ndi kuwachita. Ndipo adzakhala m'dziko ndinalipereka kwa Yakobo mtumiki wanga, limene anakhalamo makolo anu, ndipo adzakhala m'mwemo iwo, ndi ana ao, ndi zidzukulu zao kosatha; ndi Davide mtumiki wanga adzakhala mtsogoleri wao kosatha. Ndipo ndidzapangana nao pangano la mtendere, lidzakhala pangano losatha nao, ndipo ndidzawakhazika, ndi kuwachulukitsa, ndi kuika malo anga opatulika pakati pao kosatha. Kachisi wanganso adzakhala nao, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao, ndi iwo adzakhala anthu anga. Ndipo amitundu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova wakupatula Israele, pokhala pakati pao malo anga opatulika kosatha. Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti, Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako kwa Gogi, wa kudziko la Magogi, ndiye mfumu yaikulu ya Meseki ndi Tubala; nunenere motsutsana naye, uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona, nditsutsana nawe, Gogi iwe, mfumu yaikulu ya Meseki ndi Tubala; ndipo ndidzakutembenuza ndi kukowa m'chibwano mwako ndi zokowera, ndi kukutulutsa ndi nkhondo yako yonse, akavalo ndi apakavalo ovala mokwanira onsewo, msonkhano waukulu ndi zikopa zotchinjiriza, onsewo ogwira bwino malupanga; Persiya, Kusi, ndi Puti pamodzi nao, onsewo ndi chikopa ndi chisoti chachitsulo; Gomeri ndi magulu ake onse, nyumba ya Togarima, ku malekezero a kumpoto, ndi magulu ake onse, mitundu yambiri pamodzi ndi iwe. Ukonzekeretu, inde udzikonzeretu, iwe ndi msonkhano wako wonse unakusonkhanira, nukhale iwe mtsogoleri wao. Atapita masiku ambiri udzakumbukirika; zaka zotsiriza udzalowa m'dziko lobwezedwa lopulumuka lupanga, losonkhanidwa lituluke m'mitundu yambiri ya anthu, pa mapiri a Israele, amene adakhala achipululu chikhalire; koma litulutsidwa m'mitundu ya anthu, ndipo adzakhala mosatekeseka onsewo. Ndipo udzakwera udzadza ngati mkuntho, udzanga mtambo kuphimba dziko, iwe ndi magulu ako onse, ndi mitundu yambiri ya anthu pamodzi ndi iwe. Atero Ambuye Yehova, Kudzachitika tsiku ilo kuti m'mtima mwako mudzalowa zinthu, nudzalingirira chiwembu choipa, nudzati, Ndidzakwera kunka kudziko la midzi yopanda malinga, ndidzamka kwa iwo amtendere okhala mosatekeseka, onsewo akukhala opanda malinga, opanda mapiringidzo, kapena zitseko; kulanda ndi kufunkha zao, kubweza dzanja lako liononge mopasuka muli anthu tsopano, liononge mtundu wa anthu osonkhanidwa mwa amitundu, odzionera zoweta ndi chuma, okhala pakati pa dziko. Sheba, ndi Dedani, ndi amalonda a Tarisisi, ndi misona yake yonse ya mikango adzati kwa iwe, Wadza kodi kudzafunkha? Wasonkhanitsa kodi msonkhano wako kulanda, kuchoka nazo siliva ndi golide, kuchoka nazo zoweta ndi chuma, kulanda zankhondo zambiri? Chifukwa chake nenera, wobadwa ndi munthu iwe, uziti kwa Gogi, Atero Ambuye Yehova, Tsiku ilo, pokhala mosatekeseka anthu anga Israele, sudzachidziwa kodi? Ndipo udzatuluka m'malo mwako m'malekezero a kumpoto, iwe ndi mitundu yambiri ya anthu pamodzi ndi iwe, onsewo apakavalo, msonkhano waukulu ndi nkhondo yaikulu; ndipo udzakwerera anthu anga Israele ngati mtambo wakuphimba dziko; kudzachitika masiku otsiriza ndidzabwera nawe ulimbane nalo dziko langa, kuti amitundu andidziwe, pozindikiridwa Ine woyera mwa iwe, Gogi, pamaso pao. Atero Ambuye Yehova, Kodi iwe ndiwe iye amene ndinanena za iye masiku akale mwa atumiki anga aneneri a Israele, akunenera masiku aja za zaka za m'tsogolo, kuti ndidzabwera nawe kulimbana nao? Ndipo kudzachitika tsiku ilo, tsiku loti Gogi adzadza kulimbana ndi dziko la Israele, ati Ambuye Yehova, ukali wanga udzakwera m'mphuno mwanga. Pakuti ndanena mu nsanje yanga, ndi m'moto wa kuzaza kwanga, Zoonadi tsiku ilo kudzakhala kugwedezeka kwakukulu m'dziko la Israele; motero kuti nsomba za m'nyanja, ndi mbalame za m'mlengalenga, ndi nyama za kuthengo, ndi zokwawa zonse zakukwawa pansi, ndi anthu onse akukhala padziko, zidzanjenjemera pamaso panga; ndi mapiri adzagwetsedwa, ndi potsetsereka padzagumuka, ndi makoma onse adzagwa pansi. Ndipo ndidzamuitanira lupanga kumapiri anga onse, ati Ambuye Yehova, munthu aliyense lupanga lake lidzaombana nalo la mbale wake. Ndipo ndidzalimbana naye ndi mliri ndi mwazi; ndipo ndidzamvumbitsira iye, ndi magulu ake, ndi mitundu yambiri ya anthu okhala naye mvumbi waukulu, ndi matalala akulu, moto ndi sulufure. Momwemo ndidzadzikuzitsa, ndi kudzizindikiritsa woyera, ndipo ndidzadziwika pamaso pa amitundu ambiri; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu, nenera motsutsana naye Gogi, uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona, nditsutsana nawe Gogi, iwe mfumu yaikulu ya Meseki ndi Tubala; ndipo ndidzakutembenuza, ndi kukutsogolera, ndi kukweza iwe uchoke ku malekezero a kumpoto; ndipo ndidzadza nawe kumapiri a Israele; ndipo ndidzakantha uta wako kuuchotsa m'dzanja lako lamanzere, ndi kutayitsa mivi yako kudzanja lako lamanja. Udzagwa pa mapiri a Israele, iwe ndi magulu ako onse, ndi mitundu ya anthu okhala ndi iwe; ndidzakupereka kwa mbalame zolusa za mitundu yonse, ndi kwa zilombo za kuthengo, akuyese chakudya. Udzagwa kuthengo, koyera, pakuti ndanena ndine, ati Ambuye Yehova. Ndipo ndidzatumizira moto Magogi, ndi iwo okhala mosatekeseka m'zisumbu; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Ndipo ndidzadziwikitsa dzina langa loyera pakati pa anthu anga Israele, osalola dzina langa loyera aliipsenso; ndipo amitundu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Woyerayo wa Israele. Taonani, chikudza, chidzachitika, ati Ambuye Yehova, ndilo tsiku ndanenalo. Ndipo iwo okhala m'midzi ya Israele adzatuluka, nadzasonkha moto, nadzatentha zida za nkhondo, ndi zikopa zotchinjiriza, mauta, ndi mivi, ndi ndodo, ndi mikondo; ndipo adzasonkha moto nazo zaka zisanu ndi ziwiri; osatenga nkhuni kuthengo, kapena kuzitema kunkhalango; popeza adzasonkha moto ndi zidazo; nadzafunkha iwo amene anawafunkha, ndi kulanda zao za iwo adalanda zaozo, ati Ambuye Yehova. Ndipo kudzachitika tsiku ilo, ndidzapatsa Gogi manda m'Israele, chigwa cha opitawo kum'mawa kwa nyanja; ndipo lidzaletsa opitawo, ndipo adzaika komweko Gogi ndi unyinji wake wonse, nadzachitcha, Chigwa cha unyinji wa Gogi. Ndi a nyumba ya Israele adzapititsa miyezi isanu ndi iwiri alikuwaika, kuti ayeretse dziko. Inde anthu onse a m'dziko adzawaika, nadzamveka nako tsiku lakulemekezedwa Ine, ati Ambuye Yehova. Ndipo adzasankha anthu akupitapitabe m'dziko, ndi pamodzi ndi opitapitawo anthu akuika mafupa otsala pamtunda, kuliyeretsa; pakutha miyezi isanu ndi iwiri adzapwaira. Ndipo opitapitawo adzapitapita m'dziko, ndipo wina akaona fupa la munthu aikepo chizindikiro, mpaka oikawo aliika m'chigwa cha unyinji wa Gogi. Ndipo dzina la mudzi lidzakhala Hamona. Momwemo adzayeretsa dziko. Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu, atero Ambuye Yehova, Nena kwa mbalame za mitundu yonse, ndi kwa nyama zonse za kuthengo, Memezanani, idzani, sonkhanani kumbali zonse, kudza kunsembe yanga imene ndikupherani, ndiyo nsembe yaikulu pa mapiri a Israele, kuti mudzadye nyama ndi kumwa mwazi. Mudzadya nyama ya amphamvu, ndi kumwa mwazi wa akalonga a padziko, wa nkhosa zamphongo, wa anaankhosa, ndi wa mbuzi, ndi wa ng'ombe, zonsezi zonenepa za ku Basani. Ndipo mudzadya zonona mpaka mudzakhuta, ndi kumwa mwazi mpaka mudzaledzera za nsembe yanga ndakupherani. Ndipo podyera panga mudzakhuta akavalo, ndi magaleta, ndi anthu amphamvu, ndi anthu onse a nkhondo, ati Ambuye Yehova. Ndipo ndidzaika ulemerero wanga mwa amitundu; ndi amitundu onse adzaona chiweruzo changa ndachichita, ndi dzanja langa limene ndinawaikira. Ndipo nyumba ya Israele idzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, kuyambira tsiku ilo ndi m'tsogolomo. Ndipo amitundu adzadziwa kuti nyumba ya Israele idalowa undende chifukwa cha mphulupulu zao, popeza anandilakwira Ine; ndipo ndinawabisira nkhope yanga; m'mwemo ndinawapereka m'dzanja la adani ao, nagwa iwo onse ndi lupanga. Ndinachita nao monga mwa kudetsedwa kwao, ndi monga mwa kulakwa kwao, ndipo ndinawabisira nkhope yanga. Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Tsopano ndidzabweza undende wa Yakobo, ndi kuchitira chifundo nyumba yonse ya Israele, ndipo ndidzachitira dzina langa loyera nsanje. Ndipo adzasenza manyazi ao, ndi zolakwa zao zonse, zimene anandilakwira nazo, pokhala mosatekeseka iwo m'dziko lao, opanda wina wakuwaopsa; nditabwera nao kuchoka kwa mitundu ya anthu, nditawasokolotsa m'maiko a adani ao, ndi kuzindikiridwa Woyera mwa iwo pamaso pa amitundu ambiri. Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, popeza ndinalola atengedwe ndende kunka kwa amitundu, koma ndinawasonkhanitsanso akhale m'dziko lao, osasiyakonso mmodzi yense wa iwowa. Ndipo sindidzawabisiranso nkhope yanga, popeza ndatsanulira mzimu wanga pa nyumba ya Israele, ati Ambuye Yehova. Chaka cha makumi awiri ndi zisanu cha undende wathu, poyamba chaka, tsiku lakhumi lamwezi, chaka chakhumi ndi zinai atakantha mudziwo, tsiku lomwelo, dzanja la Yehova linandikhalira; ndipo anamuka nane komweko. M'masomphenya a Mulungu Iye anabwera nane m'dziko la Israele, nandikhalitsa pa phiri lalitali ndithu; pamenepo panali ngati mamangidwe a mudzi kumwera. Ndipo anamuka nane komweko, ndipo taona, panali munthu, maonekedwe ake ngati amkuwa, ndi chingwe chathonje m'dzanja lake, ndi bango loyesa nalo, naima kuchipata iye. Ndipo munthuyu anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, penya ndi maso ako, imva m'makutu mwako, nuike mtima wako pa zonse ndidzakuonetsa iwe; pakuti unatengedwa kudza kuno, kuti ndikuonetse izi; fotokozera nyumba ya Israele zonse uziona. Ndipo taonani, panali linga kunja kwake kwa nyumba ya Kachisi poizinga, ndi m'dzanja lake la munthuyo bango loyesa nalo la mikono isanu ndi umodzi, mkono uliwonse mkono kudza chikhato; ndipo anayesa chimangidwecho kuchindikira kwake bango limodzi, ndi msinkhu wake bango limodzi. Pamenepo anafika kuchipata choloza kum'mawa, nakwera pa makwerero ake; ndipo anayesa chiundo cha chipata, bango limodzi kuchindikira kwake; ndicho chiundo choyamba, bango limodzi. Ndi chipinda cha alonda, chonse ncha bango limodzi m'litali mwake, ndi bango limodzi kupingasa kwake, ndi pakati pa zipinda za alonda mikono isanu, ndi chiundo cha chipata kumbali ya kukhonde la kuchipata m'katimo, bango limodzi. Anayesanso khonde la kuchipata kumbali ya ku Kachisi, bango limodzi. Pamenepo anayesa khonde la kuchipata mikono isanu ndi itatu, ndi mphuthu zake mikono iwiri; ndi khonde la kuchipata linaloza ku Kachisi. Ndi zipinda za alonda za kuchipata cha kum'mawa ndizo zitatu chakuno, ndi zitatu chauko, zitatuzi nza muyeso umodzimodzi, ndi mphuthuzo nza muyeso umodzimodzi, chakuno ndi chauko. Ndipo anayesa kupingasa kwa chipata pakhoma pake mikono khumi, ndi utali wake wa chipata mikono khumi ndi itatu; ndi pakhomo pa zipinda za alonda panali kakhoma ka mkono umodzi chakuno, ndi kakhoma ka mkono umodzi chauko; ndi zipinda za alonda mikono isanu ndi umodzi chakuno, ndi mikono isanu ndi umodzi chauko. Ndipo anayesa chipata kuyambira kutsindwi la chipinda cha alonda chimodzi, kufikira kutsindwi la chinzake, kupingasa kwake ndiko mikono makumi awiri ndi isanu; makomo napenyana. Anamanganso nsanamira za mikono makumi asanu ndi limodzi; ndi bwalo la pakati pa chipata lidafikira kunsanamira. Ndipo kuyambira pa khomo lolowera la chipata kufikira khomo la khonde la chipata m'katimo ndiko mikono makumi asanu. Ndipo panali mazenera amkati okhazikika pazipinda ndi m'makhoma a pakati pao, m'kati mwa chipata pozungulira ponse; momwemonso pazidundumwa; ndipo panali mazenera pozungulira ponse m'katimo, ndi pa nsanamirazo panali akanjedza. Pamenepo analowa nane kubwalo lakunja, ndipo taonani, panali zipinda, ndi moyalidwa miyala mokonzekera bwalo pozungulira ponse; moyalidwa miyalamo munali zipinda makumi atatu. Ndipo moyalidwamo munali pa mbali ya zipata molingana ndi utali wake wa zipata, ndimo moyalidwa mwamunsi. Pamenepo anayesa kupingasa kwake kuyambira pakhomo pake pachipata chakunsi, kufikira kumaso kwake kwa bwalo la m'kati kunja kwake, mikono zana kum'mawa, ndi kumpoto. Ndi chipata cha bwalo lakunja choloza kumpoto anachiyesa m'litali mwake, ndi kupingasa kwake zonse mikono zana. Ndi zipinda zake ndizo zitatu chakuno, ndi zitatu chauko, ndi makhoma a pakati pake; ndi zidundumwa zake zinali monga mwa muyeso wa chipata choyambacho, m'litali mwake mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri mphambu isanu. Ndi mazenera ake, ndi zidundumwa zake, ndi akanjedza ake, anali monga mwa muyeso wa chipata choloza kum'mawa; ndipo anakwerako ndi makwerero asanu ndi awiri, ndi zidundumwa zake zinali pakhomo. Ndipo panali chipata cha bwalo lam'kati, chopenyana ndi chipata chinzake chakunja kumpoto, ndi cha kum'mawa; ndipo anayesa kuyambira kuchipata kufikira kuchipata mikono zana. Ndipo ananditsogolera kunka kumwera, ndipo taonani, panali chipata kumwera, nayesa makhoma a pakati pake, ndi zidundumwa zake, monga mwa miyeso yomweyi. Ndimo munali mazenera m'menemo, ndi m'zidundumwa zake pozungulirapo, monga mazenera ena aja, m'litali mwake mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri mphambu isanu. Ndipo panali makwerero asanu ndi awiri okwererapo, ndi zidundumwa zake kumaso kwake; ndi pa nsanamira zake chakuno ndi chauko panali akanjedza. Ndipo panali chipata cha bwalo lam'kati chakuloza kumwera, nayesa kuyambira kuchipata kufikira kuchipata kumwera mikono zana. Pamenepo analowa nane pa chipata cha kumwera m'bwalo lam'kati, nayesa chipata cha kumwera, monga mwa miyeso yomweyi; ndi zipinda zake, ndi makhoma a pakati pake, ndi zidundumwa zake, monga mwa miyeso yomweyi; ndimo munali mazenera m'menemo, ndi m'zidundumwa zake pozungulirapo; m'litali mwake mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri mphambu isanu. Ndipo panali zidundumwa pozungulirapo, m'litali mwake mikono makumi awiri mphambu isanu, ndi kupingasa kwake mikono isanu. Ndi zidundumwa zake zinaloza kubwalo lakunja, ndi pa nsanamira zake panali akanjedza, ndi pokwererapo panali makwerero asanu ndi atatu. Ndipo analowa ndine m'bwalo lam'kati kuloza kum'mawa, nayesa chipata cha kum'mawa monga mwa miyeso yomweyi; ndi zipinda zake, ndi makhoma a pakati pake, ndi zikundumwa zake, monga mwa miyeso yomweyi; ndimo munali mazenera m'menemo, ndi m'zidundumwa zake pozungulirapo, m'litali mwake mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri mphambu isanu. Ndi zidundumwa zake zinaloza kubwalo lakunja; ndi pa nsanamira zake panali akanjedza chakuno ndi chauko; ndipo pokwerera pake panali makwerero asanu ndi atatu. Pamenepo anabwera nane kuchipata cha kumpoto, nachiyesa monga mwa miyeso yomweyi; zipinda zake, makhoma a pakati pake, ndi zidundumwa zake; ndimo munali mazenera m'menemo pozungulirapo, m'litali mwake mikono makumi asanu, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri mphambu isanu. Ndi nsanamira zake zinaloza kubwalo lakunja; ndi pa nsanamira zake panali akanjedza chakuno ndi chauko; ndipo pokwerera pake panali makwerero asanu ndi atatu. Ndipo pa nsanamira za pazipata panali kanyumba ndi chitseko chake; pamenepo anatsuka nsembe yopsereza. Ndipo m'khonde la pachipata munali magome awiri chakuno, ndi magome awiri chauko, kuti apherepo nsembe yopsereza, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula. Ndi kumbali ina ya khonde kunja, pakukwerera polowera pa chipata cha kumpoto, kunali magome awiri, ndi kumbali inzake ya kuchipata kunali magome awiri. Magome anai chakuno, ndi magome anai chauko, kumbali ya chipata; magome asanu ndi atatu, amene anapherapo nsembe. Ndipo panali magome anai a nsembe yopsereza a miyala yosema, m'litali mwake mkono ndi nusu, kupingasa kwake mkono ndi nusu, msinkhu wake mkono umodzi; pamenepo ankaika zipangizo zimene anaphera nazo nsembe yopsereza ndi nsembe yophera. Ndi zichiri zangowe, chikhato m'litali mwake, zinamangika m'katimo pozungulirapo; ndi pamagome panali nyama ya nsembe. Ndi kunja kwa chipata cha m'kati kunali tinyumba ta oimba m'bwalo lam'kati, kumbali ya chipata cha kumpoto; ndipo tinaloza kumwera, kena kumbali ya chipata cha kum'mawa kanaloza kumpoto. Ndipo anati kwa ine, Kanyumba aka koloza kumwera nka ansembe odikira Kachisi. Ndi kanyumba koloza kumpoto nka ansembe odikira guwa la nsembe, ndiwo ana a Zadoki amene ayandikira kwa Yehova mwa ana a Levi, kumtumikira Iye. Ndipo anayesa bwalolo mikono zana m'litali mwake, ndi mikono zana kupingasa kwake, laphwamphwa; ndi guwa la nsembe linali kukhomo kwa nyumba. Pamenepo anadza nane kukhonde la Kachisi, nayesa mphuthu za khonde, mikono isanu chakuno, ndi mikono isanu chauko; ndi kupingasa kwa chipata, mikono itatu chakuno, ndi mikono itatu chauko. M'litali mwake mwa khonde mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwake mikono khumi ndi umodzi; ndipo panali makwerero khumi okwerera kumeneko; ndipo panali zoimiritsa pa nsanamirazo, imodzi chakuno, ndi imodzi chauko. Ndipo anadza nane ku Kachisi, nayesa nsanamira zake, kupingasa kwake mikono isanu ndi umodzi chakuno, ndi mikono isanu ndi umodzi chauko, ndiko kupingasa kwa chihema chija. Ndi kupingasa kwa khomo mikono khumi; ndi mbali za khomo mikono isanu chakuno, ndi mikono isanu chauko; nayesa malo opatulika, m'litali mwake mikono makumi anai, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri. Nalowa m'katimo, nayesa mphuthu za pakhomo mikono iwiri, ndi msinkhu wa khomo mikono isanu ndi umodzi, ndi kupingasa kwa khomo mikono isanu ndi iwiri. Anayesanso m'kati mwa Kachisi m'tsogolomo, m'litali mwake mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri; ndipo anati kwa ine, Umo m'mopatulika kwambiri. Pamenepo anayesa khoma la nyumba, kuchindikira kwake mikono isanu ndi umodzi, ndi kupingasa kwake kwa zipinda za m'mphepete mikono inai, pozungulira pake ponse pa Kachisi. Ndipo zipinda za m'mphepete zinasanjikizana china pa chinzake; zinatero makumi atatu mizere yonse itatu, nizinalowa kukhoma lochirikiza zipinda za m'mphepete pozungulirapo, zisanjikike pamenepo; pakuti sizinagwiridwa ndi khoma la nyumba. Ndipo zipinda za m'mphepete zinakula m'kupingasa kwao, pozinga nyumba m'kukwera kwao; pakuti nyumba inazingika mokwerakwera pozungulira pake pa nyumba; motero kupingasa kwake kwa nyumba kunakula kumwamba kwake, momwemonso anakwera kuyambira chipinda chakunsi, kupita chapakati, kufikira cham'mwamba. Ndinaonanso kuti kunyumba kunali chiunda pozungulira pake; maziko a zipinda za m'mphepete anafikira muyeso wa bango la mikono isanu ndi umodzi yaikulu. Kuchindikira kwa khoma la kuzipinda za m'mphepete kunja kwake kunali mikono isanu; ndipo mpata wake unali malo olowera m'zipinda za m'mphepete za Kachisi. Ndi pakati pa zipinda panali kupingasa kwa mikono makumi awiri, pozungulira pake ponse pa nyumba. Ndi makomo a zipinda za m'mphepete analoza kumpatawo, khomo lina kumpoto, ndi lina kumwera; ndi malo a pa mpatawo anayesa mikono isanu kupingasa kwake pozungulira pake. Ndipo nyumba inali kutsogolo kwa mpata wa mbali ya kumadzulo inali ya mikono makumi asanu ndi awiri kupingasa kwake; ndi khoma la nyumbayo pozungulira pake linali la mikono isanu kuchindikira kwake; ndi m'litali mwake mikono makumi asanu ndi anai. Momwemo anayesa Kachisi m'litali mwake mikono zana limodzi; ndi mpatawo, ndi nyumbayo, ndi makoma ake, mikono zana limodzi; kupingasa kwake komwe kwa kukhomo kwa nyumba, ndi kumpatawo kum'mawa, mikono zana limodzi. Momwemo anayesa m'litali mwake nyumbayo inali kutsogolo kwake kwa mpata wokhala chakuno chake, ndi makonde ake am'mwamba, chakuno ndi chauko, mikono zana limodzi, ndi Kachisi wa m'katimo, ndi makonde a kubwalo; ziundo, ndi mazenera amkati okhazikika, ndi makonde am'mwamba akuzinga zipinda zosanjikizana zao zitatu, pandunji pa chiundo, otchinga ndi matabwa pozungulira pake, kuyambira pansi kufikira kumazenera; koma mazenera anaphimbika; kufikira kumwamba pa khomo, mpaka nyumba ya m'katimo, ndi kunja kwake, ndi khoma lonse kwete m'kati ndi kunja, monga mwa miyeso. Ndipo panalembedwapo ndi akerubi ndi akanjedza, kanjedza pakati pa akerubi; ndi kerubi aliyense anali ndi nkhope zake ziwiri; nkhope ya munthu kuloza kukanjedza chakuno, ndi nkhope ya mwanawamkango kuloza kukanjedza chauko, momwemo m'nyumba monse pozungulira pake. Kuyambira pansi kufikira pamwamba pa khomo panalembedwa akerubi ndi akanjedza; linatero khoma la Kachisi. Mphuthu za Kachisi zinali zaphwamphwa, ndi maonekedwe a pakhomo pa malo opatulika ananga maonekedwe a Kachisi. Guwa la nsembe linali lamtengo, msinkhu wake mikono itatu, ndi m'litali mwake mikono iwiri, ndi ngodya zake, ndi tsinde lake, ndi thupi, nza mtengo; ndipo ananena ndi ine, Ili ndiko gome lili pamaso pa Yehova. Ndipo Kachisi ndi malo opatulika kwambiri anali nazo zitseko ziwiri. Ndipo pamakomopo panali zitseko zopatukana zotembenuzika, china chopatukana pa khomo lina china pa linzake. Ndipo panalembedwa pamenepo pa zitseko za Kachisi akerubi ndi akanjedza, akunga aja adalembedwa pamakoma; ndipo panali matabwa ochindikira pakhomo pakhonde panja. Ndipo panali mazenera amkati okhazikika, ndi akanjedza chakuno ndi chauko, kumbali zake za khonde; momwemonso pa zipinda za m'mphepete mwa nyumba, ndi pa matabwa ochindikira. Pamenepo anatuluka nane kunka kubwalo la kunja, njira ya kumpoto; nalowa nane kunyumba yazipinda idali pandunji pa mpatawo, ndi pandunji pa nyumbayo inaloza kumpoto. Chakuno cha m'litali mwake mwa mikono zana limodzi kunali khomo la kumpoto, ndi kupingasa kwake mikono makumi asanu. Pandunji pa mikono makumi awiri a bwalo lam'kati, ndi pandunji pa moyalamo mwa miyala, mwa bwalo lakunja, panali khonde lam'mwamba, lokomana ndi khonde linzake losanjikika pachiwiri. Ndi kukhomo kwa zipinda anakonza poyendapo, kupingasa kwake mikono khumi m'kati mwake, njira ya mikono zana limodzi, ndi makomo ao analoza kumpoto. Ndipo zipinda zapamwamba zinachepa, pakuti makonde am'mwamba analanda pamenepo, chifukwa chake zinachepa koposa zapansi ndi zapakati m'nyumba yazipinda. Pakuti zinasanjikizana pawiri, ndipo zinalibe nsanamira ngati nsanamira za kumabwalo; chifukwa chake zam'mwambazo zinachepa koposa zakunsi ndi pakati kuyambira pansi. Ndipo linga linali kunjalo, lolingana ndi nyumba yazipinda, kuloza kubwalo lakunja, popenyana ndi nyumba yazipinda, m'litali mwake munali mikono makumi asanu. Pakuti kupingasa kwake kwa nyumba yazipinda inali m'bwalo lakunja, kunali mikono makumi asanu; ndipo taonani, kuloza kukhomo la Kachisi inali mikono zana limodzi. Ndipo pansi pa zipinda izi panali polowera mbali ya kum'mawa, poloweramo kuchoka kubwalo lakunja. M'kuchindikira kwa linga la bwalo, kuloza kumwera, chakuno cha mpatawo, chakuno cha nyumba, panali nyumba yazipinda. Ndipo njira ya pakhomo pao inanga maonekedwe njira ya kunyumba yazipinda yoloza kumpoto, inalingana nayo m'litali mwake, momwemonso kupingasa kwake; ndi m'matulukiro mwake monse munali monga mwa machitidwe a inzake, ndi monga mwa makomo a inzake. Ndi monga mwa makomo a zipinda za kumwera panali khomo polekeza njira, ndiyo njira yokhudzana ndi linga la kum'mawa polowamo. Pamenepo anati kwa ine, Zipinda za kumpoto, ndi zipinda za kumwera, zili chakuno cha mpatawo, ndizo zipinda zopatulika, kumene ansembe okhala pafupi pa Yehova azidyera zinthu zopatulika kwambiri; kumeneko aziika zopatulika kwambiri, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula; pakuti malowo ndi opatulika. Atalowa ansembe asatulukenso m'malo opatulika kunka kubwalo lakunja, koma komweko aziika zovala zao zimene atumikira nazo; pakuti zili zopatulika; ndipo avale zovala zina, nayandikire zinthu wamba za anthu. Atatha tsono kuyesa nyumba ya m'katimo, anatuluka nane njira ya chipata choloza kum'mawa nayesa bwalo pozungulira pake. Anayesa mbali ya kum'mawa, ndi bango loyesera, mikono mazana asanu, kuyesa ndi bango loyesera. Anayesa mbali ya kumpoto mikono mazana asanu, kuyesa ndi bango loyesera. Anayesa mbali ya kumwera mikono mazana asanu, kuyesa ndi bango loyesera. Anatembenukira kumbali ya kumadzulo, nayesa mikono mazana asanu ndi bango loyesera. Analiyesa mbali zake zinai, linali nalo linga pozungulira pake, utali wake mikono mazana asanu, chitando chake mikono mazana asanu, kusiyanitsa pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba. Pamenepo anamuka nane kuchipata choloza kum'mawa, ndipo taonani, ulemerero wa Mulungu wa Israele unadzera njira ya kum'mawa, ndi mau ake ananga mkokomo wa madzi ambiri, ndi dziko linanyezimira ndi ulemerero wake. Ndipo maonekedwe a masomphenya ndinawaona anali monga masomphenya aja ndinawaona pakudza ine kupasula mudzi; ndi masomphenyawa anali ngati masomphenya aja ndinawaona kumtsinje wa Kebara; ndipo ndinagwa nkhope pansi. Ndipo ulemerero wa Yehova unalowa m'Kachisi kudzera njira ya chipata choloza kum'mawa. Ndipo mzimu unandinyamula numuka nane kubwalo la m'kati; ndipo taonani, ulemerero wa Yehova unadzaza Kachisi. Ndipo ndinamva wina alikulankhula nane ali m'Kachisi, naima nane munthu. Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, pano mpokhala mpando wachifumu wanga, mpoponda kumapazi anga, pomwe ndidzakhala pakati pa ana a Israele kosatha; ndi nyumba ya Israele siidzadetsanso dzina langa loyera, ngakhale iwo kapena mafumu ao, mwa chigololo chao, ndi mitembo ya mafumu ao pa misanje yao, ndi kuika chiundo chao pafupi pa chiundo changa, ndi mphuthu yao pa mbali ya mphuthu yanga, ndipo panali khoma lokha pakati pa iwo ndi Ine, nadetsa dzina langa loyera ndi zonyansa zao anazichita; chifukwa chake ndinawatha mu mkwiyo wanga. Ataye tsono chigololo chao ndi mitembo ya mafumu ao kutali kwa Ine, ndipo ndidzakhala pakati pao kosatha. Wabadwa ndi munthu iwe, onetsa nyumba ya Israele Kachisiyu, kuti achite manyazi ndi mphulupulu zao; ndipo ayese muyeso wake. Ndipo ngati akachita manyazi nazo zonse anazichita, uwadziwitse maonekedwe a Kachisiyu, ndi muyeso wake, ndi potulukira pake, ndi polowera pake, ndi malongosoledwe ake onse, ndi malemba ake onse, ngakhale maonekedwe ake onse, ndi malamulo ake onse; nuwalembere pamaso pao, kuti asunge maonekedwe ake onse, ndi malemba ake onse, nawachite. Lamulo la Kachisi ndi ili: pamwamba pa phiri malire ake onse pozungulira pake azikhala opatulika kwambiri. Taonani, limeneli ndi lamulo la Kachisi. Ndipo miyeso ya guwa la nsembe, kuyesa mikono ndi iyi: (mkonowo ndiwo mkono ndi chikhato), tsinde lake likhale mkono, ndi kupingasa kwake dzanja limodzi, ndi mkuzi wake m'mphepete mwake pozungulira pake kuyesa zala; ili ndi tsinde la guwali. Ndi kuyambira kunsi kwake kunthaka, kufikira phaka lamunsi, mikono iwiri; ndi kupingasa kwake mkono umodzi; ndi kuyambira phaka laling'ono kufikira phaka lalikulu mikono inai; ndi kupingasa kwake mkono. Ndi guwa lapamwamba mikono inai; ndi pamoto pa guwa padzatuluka nyanga zinai. Ndi pamoto pa guwa, m'litali mwake mikono khumi ndi iwiri, ndi kupingasa kwake khumi ndi iwiri, laphwamphwa mbali zake zinai. Ndi phaka, m'litali mwake mikono khumi ndi inai, ndi kupingasa kwake mikono khumi ndi inai kumbali zake zinai; ndi mkuzi wake pozungulira pake mkono wa nusu, ndi tsinde lake mkono pozungulira pake, ndi makwerero ake aloza kum'mawa. Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, atero Ambuye Yehova, Malemba a guwa la nsembe, tsiku lakulimanga, kuperekapo nsembe zopsereza, ndi kuwazapo mwazi, ndi awa; Upatse ansembe Alevi, a mbeu za Zadoki, okhala pafupi ndi Ine, kunditumikira Ine, ati Ambuye Yehova, mwanawang'ombe, akhale wa nsembe yauchimo. Nutengeko mwazi wake, ndi kupaka pa nyanga zinai za guwa, ndi pangodya zinai za phaka, ndi pa mkuzi wake pozungulira; motero uliyeretse ndi kulichitira chotetezera. Utengenso ng'ombe ya nsembe yauchimo, aipsereze pa malo oikika a Kachisi kunja kwa malo opatulika. Ndipo tsiku lachiwiri upereke tonde wopanda chilema, akhale nsembe yauchimo; ndipo ayeretse guwa la nsembe monga umo analiyeretsera ndi ng'ombeyo. Utatha kuliyeretsa upereke mwanawang'ombe wopanda chilema, ndi nkhosa yamphongo ya zoweta yopanda chilema. Ndipo ubwere nazo kwa Yehova, ndi ansembe athirepo mchere, ndi kuzipereka nsembe yopsereza ya Yehova. Masiku asanu ndi awiri uzikonzera mbuzi tsiku ndi tsiku, ikhale nsembe yauchimo; akonzerenso mwanawang'ombe, ndi nkhosa yamphongo ya zoweta zopanda chilema. Masiku asanu ndi awiri achite chotetezera guwali ndi kuliyeretsa, momwemo alipatule. Ndipo atatsiriza masiku, kudzachitika tsiku lachisanu ndi chitatu ndi m'tsogolo, ansembe azichita nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zoyamika pa guwalo; ndipo ndidzakulandirani, ati Ambuye Yehova. Pamenepo anandibweza njira ya kuchipata chakunja cha malo opatulika choloza kum'mawa, koma chinatsekedwa. Ndipo Yehova anati kwa ine, Chipata ichi chitsekeke, chisatseguke, osalowako munthu; pakuti Yehova Mulungu wa Israele walowerapo; chifukwa chake chitsekeke. Koma kunena za kalonga, iye akhale m'menemo monga kalonga kudya mkate pamaso pa Yehova; alowe kunjira ya kukhonde la chipata, natulukire njira yomweyi. Atatero anamuka nane njira ya chipata cha kumpoto kukhomo kwa Kachisi, ndipo ndinapenya, taonani, ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehova; pamenepo ndinagwa nkhope pansi. Ndipo Yehova anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, samalira bwino, nupenye ndi maso ako, numve m'makutu mwako zonse ndidzanena nawe, kunena za malemba onse a nyumba ya Yehova, ndi malamulo ake onse; nusamalire bwino malowedwe a nyumbayi, ndi matulukidwe ake onse a malo opatulika. Nunene kwa opandukawo, kwa nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Nyumba ya Israele inu, Zikukoleni zonyansa zanu zonse; popeza mwalowa nao achilendo osadulidwa m'mtima, osadulidwa m'thupi akhale m'malo anga opatulika kuwadetsa, ndiwo nyumba yanga, popereka inu mkate wanga, mafuta, ndi mwazi; ndipo munathyola pangano langa pamodzi ndi zonyansa zanu zonse. Ndipo simunasunga udikiro wa zopatulika zanga, koma mwadziikira mokha osunga udikiro wanga m'malo anga opatulika. Atero Ambuye Yehova, Palibe mlendo wosadulidwa m'mtima, wosadulidwa m'thupi, alowe m'malo anga opatulika, mwa alendo onse ali pakati pa ana a Israele. Koma Aleviwo anandichokera kunka kutaliwo, posokera Israele, amene anandisokerera ndi kutsata mafano ao, iwowa adzasenza mphulupulu yao. Koma adzakhala atumiki m'malo anga opatulika, akuyang'anira kuzipata za Kachisi, ndi kutumikira m'Kachisimo, aziwaphera anthu nsembe yopsereza, ndi nsembe yophera, naime pamaso pao kuwatumikira. Popeza anawatumikira pamaso pa mafano ao, nakhala chokhumudwitsa cha mphulupulu cha nyumba ya Israele, chifukwa chake ndawakwezera dzanja langa, ati Ambuye Yehova; ndipo adzasenza mphulupulu yao. Ndipo asayandikire kwa Ine kundigwirira ntchito ya nsembe, kapena kuyandikira zopatulika zanga zilizonse zopatulika kwambirizo; koma azisenza manyazi ao, ndi zonyansa zao anazichita. Koma ndidzawaika akhale osunga udikiro wa Kachisi kwa utumiki wake wonse, ndi zonse zakumachitika m'mwemo. Koma ansembe Alevi, ana a Zadoki, akusunga udikiro wa malo anga opatulika pondisokerera ana a Israele, iwowa adzandiyandikira kunditumikira Ine, nadzaima pamaso panga, kupereka mafuta ndi mwazi kwa Ine, ati Ambuye Yehova; iwowa adzalowa m'malo anga opatulika, nadzayandikira kugome langa kunditumikira, nadzasunga udikiro wanga. Ndipo kudzatero, polowa iwo kuzipata za bwalo lam'kati avale zovala zabafuta; koma zaubweya asazivale ponditumikira Ine m'zipata za bwalo la m'kati, ndi m'Kachisi. Akhale nao akapa abafuta pamitu pao, ndi akabudula m'chuuno mwao; asavale m'chuuno kanthu kalikonse kakuchititsa thukuta. Ndipo akatulukira kubwalo lakunja, kubwalo lakunja kuli anthu, azivula zovala zao zimene atumikira nazo, naziike m'zipinda zopatulika, navale zovala zina; angapatule anthu ndi zovala zao. Ndipo asamete mitu yao, kapena asalekerere nzera za tsitsi lao zikule, azingoyepula tsitsi la mitu yao. Kungakhale kumwa vinyo, wansembe asamwe polowa kubwalo la m'katimo. Kungakhale kutenga amasiye kapena osudzulidwa akhale akazi ao, asachite; koma atenge anamwali a mbeu ya nyumba ya Israele, kapena wamasiye ndiye wamasiye wa wansembe. Ndipo aziphunzitsa anthu anga asiyanitse pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba, ndi kuwazindikiritsa pakati pa zodetsa ndi zoyera. Ndipo pakakhala mlandu, aimeko kuweruza; auweruze monga mwa maweruzo anga, ndipo azisunga malamulo anga, ndi malemba anga, pazikondwerero zanga zonse zoikika; napatulikitse masabata anga. Ndipo asayandikire kwa munthu aliyense wakufa, angadzidetse; koma chifukwa cha atate, kapena mai, kapena mwana wamwamuna, kapena mwana wamkazi, kapena mbale, kapena mlongo wopanda mwamuna, nkuloleka kudzidetsa. Ndipo atayeretsedwa amwerengere masiku asanu ndi awiri. Ndipo tsiku loti alowa m'malo opatulika, bwalo lam'kati, kutumikira m'malo opatulika, apereke nsembe yake yauchimo, ati Ambuye Yehova. Ndipo adzakhala nacho cholowa; Ine ndine cholowa chao; musawapatsa cholandira chao m'Israele; Ine ndine cholandira chao. Azidya nsembe yaufa, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula; ndipo zilizonse zoperekedwa chiperekere m'Israele ndi zao. Ndi zoyamba za zipatso zoyamba za zinthu zilizonse, ndi nsembe zokweza zilizonse za nsembe zanu zonse zokweza nza ansembe; muperekenso ufa wanu woyamba kwa wansembe, kuti mdalitso ukhalebe pa nyumba yako. Ansembe asadyeko kanthu kakufa kokha, kapena kogwidwa ndi chilombo, ngakhale mbalame, kapena nyama. Ndipo pogawa dziko likhale cholowa chao, mupereke chopereka kwa Yehova, ndicho gawo lopatulika la dziko; m'litali mwake likhale la mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu, ndi kupingasa kwake mikono zikwi makumi awiri; likhale lopatulika m'malire ake onse pozungulira pake. Kutengako malo opatulika akhale nayo mikono mazana asanu m'litali mwake, ndi mazana asanu kupingasa kwake, laphwamphwa pozungulira pake; ndi pabwalo pake poyera pozungulira pake mikono makumi asanu. Ndipo kuyambira poyesedwapo uyese mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwake, ndi mikono zikwi khumi kupingasa kwake; m'menemo ndimo mukhale malo opatulika, ndiwo opatulika, ndiwo opatulika kwambiri. Ndilo gawo lopatulika la dziko, ndilo la ansembe atumiki a malo opatulika, amene ayandikira kutumikira Yehova; apo ndipo amange nyumba zao, likhale malo a pa okha a kwa malo opatulika. Ndipo mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwake, ndi mikono zikwi khumi kupingasa kwake, ndilo gawo la Alevi, atumiki a Kachisi; likhale laolao la midzi yokhalamo. Ndipo dziko lake la mudziwo mulipereke la mikono zikwi zisanu kupingasa kwake, ndi mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwake, pa mbali ya chipereko chopatulika, ndilo la nyumba yonse ya Israele. Ndipo kalonga adzakhala nalo gawo lake mbali ina ndi mbali inzake ya chipereko chopatulika, ndi ya dziko la mudzi, kutsogolo kwa chipereko chopatulika, ndi kutsogolo kwa dziko la mudzi, mbali ya kumadzulo, ndi mbali ya kum'mawa; ndi m'litali mwake mudzalingana ndi limodzi la magawo, kuyambira kumalire a kumadzulo kufikira malire a kum'mawa. M'dzikomo ili lidzakhala lakelake m'Israele; ndipo akalonga anga sadzazunzanso anthu anga, koma adzapereka dziko kwa nyumba ya Israele monga mwa mafuko ao. Atero Ambuye Yehova, Likufikireni akalonga a Israele inu, lekani kuchita chiwawa, ndi kulanda za eni ake; muchite chiweruzo ndi chilungamo; lekani kupirikitsa anthu anga m'zolowa zao, ati Ambuye Yehova. Muzikhala nayo miyeso yoona, ndi efa woona, ndi bati loona. Efa ndi bati zikhale za muyeso umodzi, bati liyese limodzi la magawo khumi la homeri, efa lomwe liyese limodzi la magawo khumi la homeri; muyeso wao uyesedwa monga mwa homeri. Ndipo sekeli ndilo magera makumi awiri; masekeli makumi awiri, ndi masekeli awiri ndi asanu, ndi masekeli khumi ndi asanu, ndiwo muyeso wa mina wanu. Chopereka muchipereke ndicho limodzi la magawo asanu ndi limodzi la efa, kulitapa pa homeri wa tirigu; muperekenso limodzi la magawo asanu ndi limodzi la efa, kulitapa pa homeri wa barele; ndi gawo lonenedwa la mafuta, la bati wa mafuta, ndilo limodzi la magawo khumi la bati, kulitapa pa kori; ndiwo mabati khumi, ndiwo homeri; pakuti mabati khumi ndiwo homeri; ndi mwanawankhosa mmodzi wa zoweta, kumtenga pa mazana awiri wochokera kumadimba a Israele, ndiye wa nsembe yaufa, ndi wa nsembe yopsereza, ndi wa nsembe zoyamika, kuwachitira chotetezera, ati Ambuye Yehova. Anthu onse a m'dziko azipereka chopereka ichi chikhale cha kalonga wa m'Israele. Ndipo udindo wa kalonga ndiwo kupereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi nsembe zothira, pachikondwerero, ndi pokhala mwezi, ndi pa masabata; pa zikondwerero zonse zoikika a nyumba ya Israele; ndipo apereke nsembe yauchimo, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yopsereza, ndi nsembe zamtendere, kuchitira chotetezera nyumba ya Israele. Atero Ambuye Yehova, Mwezi woyamba, tsiku loyamba la mwezi, uzitenga mwanawang'ombe wopanda chilema, ndipo uyeretse malo opatulika. Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yauchimo, naupake pa mphuthu za Kachisi, ndi pangodya zinai za phaka la guwa la nsembe, ndi pa mphuthu za chipata cha bwalo lam'kati. Tsiku lachisanu ndi chiwiri la mweziwo uchitire momwemo aliyense wolakwa ndi wopusa; motero muchitire Kachisiyo chomtetezera. Mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi, muzichita Paska, chikondwerero cha masiku asanu ndi awiri; audye mkate wopanda chotupitsa. Ndipo tsiku lomwelo kalonga adzikonzere yekha ndi anthu onse a m'dziko ng'ombe, ikhale ya nsembe yauchimo. Ndipo masiku asanu ndi awiri a chikondwerero akonzere Yehova nsembe yopsereza, ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri zopanda chilema, tsiku ndi tsiku, masiku asanu ndi awiriwa; ndi tonde tsiku ndi tsiku, akhale wa nsembe yauchimo. Nakonze nsembe yaufa, kung'ombe kukhale efa; ndi kunkhosa yamphongo kukhale efa; ndi kuefa kukhale hini wa mafuta. Mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi, pachikondwerero, achite momwemo masiku asanu ndi awiri, monga mwa nsembe yauchimo, monga mwa nsembe yopsereza, ndi monga mwa nsembe yaufa, ndi monga mwa mafuta. Atero Ambuye Yehova, Pa chipata cha bwalo lam'kati choloza kum'mawa patsekedwe masiku asanu ndi limodzi ogwira ntchito; koma tsiku la Sabata patsegulidwe, ndi tsiku lokhala mwezi patsegulidwe. Ndipo kalonga azilowera njira ya kukhonde la chipatacho, kunja kwake, naime kunsanamira ya chipata; ndipo ansembe akonze nsembe yake yopsereza, ndi nsembe zake zoyamika, nalambire iye kuchiundo cha chipata; atatero atuluke; koma pachipata pasatsekedwe mpaka madzulo. Ndipo anthu a m'dziko alambire pa chitseko cha chipata ichi pamaso pa Yehova pamasabata, ndi pokhala mwezi. Ndipo nsembe yopsereza imene kalonga azipereka kwa Yehova pa Sabata ndiyo anaankhosa asanu ndi mmodzi opanda chilema, ndi nkhosa yamphongo yopanda chilema, ndi nsembe yaufa ikhale efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi nsembe ya ufa wa pa anaankhosa, monga akhoza kupatsa; ndi hini wa mafuta wa paefa. Ndipo nsembe ya tsiku lokhala mwezi ikhale mwanawang'ombe wopanda chilema, ndi anaankhosa asanu ndi mmodzi, ndi nkhosa yamphongo, zikhale zopanda chilema; ndipo akonze nsembe yaufa, efa wa pa ng'ombe, ndi efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi pa anaankhosa, monga akhoza; ndi hini wa mafuta wa paefa. Ndipo polowa kalonga azilowera njira ya kukhonde la chipata, natuluke njira yomweyo. Koma pofika anthu a m'dziko pamaso pa Yehova m'zikondwerero zoikika, iye amene alowera njira ya kuchipata cha kumpoto kudzalambira, atulukire njira ya kuchipata cha kumwera; ndi iye amene alowera njira ya kuchipata cha kumwera, atulukire njira ya kuchipata cha kumpoto; asabwerere njira ya chipata anadzeracho, koma atulukire m'tsogolo mwake. Kalongayo tsono, polowa iwo alowe pakati pao, ndipo potuluka iwo atulukire pamodzi. Ndi pazikondwerero, ndi pa masiku opatulika, nsembe yaufa ikhale ya efa wa pa ng'ombe, ndi efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi pa anaankhosa, monga akhoza kupatsa; ndi hini wa mafuta wa paefa. Ndipo kalonga akapereka chopereka chaufulu nsembe yopsereza, kapena nsembe zoyamika kwa Yehova, amtsegulire pa chipata choloza kum'mawa; ndipo azipereka nsembe yake yopsereza, ndi nsembe zake zoyamika, monga umo amachitira tsiku la Sabata; atatero atuluke; ndipo atatuluka, wina atseke pachipata. Uziperekanso kwa Yehova mwanawankhosa wa chaka chimodzi akhale nsembe yopsereza wopanda chilema, tsiku ndi tsiku, m'mawa ndi m'mawa, uzimpereka. Uperekenso nsembe yaufa pamodzi naye m'mawa ndi m'mawa, limodzi la magawo asanu ndi limodzi la efa, ndi limodzi la magawo atatu la hini wa mafuta, kusanganiza ndi ufa wosalala, ndiyo nsembe yaufa ya Yehova kosalekeza, mwa lemba losatha. Momwemo apereke mwanawankhosa, ndi nsembe yaufa, ndi mafuta, m'mawa ndi m'mawa, nsembe yopsereza kosalekeza. Atero Ambuye Yehova, Kalonga akapatsa mwana wake wina wamwamuna mphatso idzakhala cholowa chake, ndicho chaochao cha ana ake, cholowa chao. Koma akapatsa mphatso yotenga kucholowa chake kwa wina wa anyamata ake, idzakhala yake mpaka chaka cha ufulu; pamenepo ibwerere kwa kalonga, koma cholowa chake chikhale cha ana ake. Ndipo kalonga asatengeko cholowa cha anthu kuwazunza, ndi kulanda dziko laolao; apatse ana ake cholowa kulemba dziko lakelake, kuti anthu anga asabalalike, yense kuchoka m'dziko lake. Pamenepo anapita ndi ine podzera paja pali kumbali ya chipata kunka kuzipinda zopatulika za ansembe zoloza kumpoto; ndipo taonani, kunali malo chauko kumadzulo. Ndipo anati kwa ine, Pano ndipo ansembe aziphikira nsembe yopalamula, ndi nsembe yauchimo; kumenenso aziocha mikate ya ufa wa nsembe, kuti asatuluke nazo kubwalo lakunja ndi kupatulika kwambiri anthu, Pamenepo anatulukira nane kubwalo lakunja, nandipititsa kungodya zinai za bwaloli; ndipo taonani, m'ngodya monse munali bwalo. M'ngodya zinai za bwalo munali mabwalo ochingika, m'litali mwake mikono makumi anai, kupingasa kwake makumi atatu; awa anai m'ngodyazi analingana muyeso wake. Ndipo panali maguwa pozungulira pake m'menemo, pozungulira pake pa mabwalo anai; ndipo anamanga maguwawo ndi mafuwa pansi pake pozungulirapo. Ndipo anati kwa ine, Izi ndi nyumba zophikiramo, kumene atumiki a Kachisi aziphikira nsembe ya anthu. Ndipo anandibwezera ku khomo la nyumba, ndipo taonani, panatumphuka madzi pansi pa chiundo cha nyumba kum'mawa; pakuti khomo lake la nyumba linaloza kum'mawa; ndipo madzi anatsika kuchokera pansi pa nyumba, kumbali ya lamanja lake, kumwera kwa guwa la nsembe. Pamenepo anatuluka nane njira ya kuchipata cha kumpoto, nazungulira nane njira yakunja kunka kuchipata chakunja, njira ya kuchipata choloza kum'mawa; ndipo taonani, panatuluka madzi pa mbali ya kulamanja. Potuluka munthuyu kunka kum'mawa ndi chingwe choyesera m'dzanja lake, anayesa mikono chikwi chimodzi, nandipititsa pamadzi, madzi oyesa m'kakolo. Nayesanso chikwi chimodzi, nandipititsa pamadzi, madzi oyesa m'maondo. Nayesanso chikwi chimodzi, nandipititsa pamadzi, madzi oyesa m'chuuno. Atatero anayesanso chikwi chimodzi, ndipo mtsinje wosakhoza kuoloka ine, popeza madzi adakula, madzi osambira, mtsinje wosaoloka munthu. Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, waona ichi? Nanditenga kundikwezetsa ndi mtsinje. Nditabwera tsono, taonani, pa gombe la mtsinjewo mitengo yambirimbiri tsidya lino ndi lija. Pamenepo anati kwa ine, Madzi awa atulukira kudera la kum'mawa, natsikira kuchidikha, nayenda kunyanja; atathira kunyanja akonzeka madzi ake. Ndipo kudzatero kuti zamoyo zonse zochuluka zidzakhala ndi moyo kulikonse mtsinjewo ufikako, ndi nsomba zidzachuluka kwambiri; pakuti madzi awa anafikako, nakonzeka madzi a m'nyanja; ndipo kulikonse mtsinje ufikako zilizonse zidzakhala ndi moyo. Ndipo kudzachitika, kuti asodzi adzaima komweko; kuyambira pa Engedi kufikira ku Enegilaimu kudzakhala poyanikira makoka; nsomba zao zidzakhala za mitundumitundu, ngati nsomba za m'Nyanja Yaikulu, zambirimbiri. Koma pali matope ake ndi zithaphwi zake sipadzakonzeka, paperekedwa pakhale pamchere. Ndipo kumtsinje, kugombe kwake tsidya lino ndi lija, kudzamera mtengo uliwonse wa chakudya, osafota tsamba lake, zipatso zake zomwe zosasowa; idzabala zipatso zatsopano mwezi ndi mwezi, popeza madzi ake atumphuka m'malo opatulika; ndi zipatso zake zidzakhala chakudya, ndi tsamba lake lakuchiritsa. Atero Ambuye Yehova, Malire amene mugawe nao dziko likhale cholowa chao monga mwa mafuko khumi ndi awiri a Israele ndi awa: Yosefe akhale nao magawo awiri. Ndipo mudzakhala nalo cholowa chanu wina ndi mnzake yemwe, ndilo limene ndinakwezapo dzanja langa kulipereka kwa makolo anu, ndi dziko ili lidzakugwerani cholowa chanu. Ndipo malire a dzikoli ndi awa: mbali ya kumpoto, kuyambira ku Nyanja Yaikulu, kutsata njira ya ku Hetiloni, kufikira polowera ku Zedadi; Hamati, Berota, Sibraimu, ndiwo pakati pa malire a Damasiko, ndi malire a Hamati; Hazere-Hatikoni ndiwo kumalire a Haurani. Ndi malire ochokera kunyanja ndiwo Hazar-Enoni, kumalire a Damasiko, ndi kumpoto kulinga kumpoto kuli malire a Hamati. Ndiyo mbali ya kumpoto. Ndi mbali ya kum'mawa pakati pa Haurani, ndi Damasiko, ndi Giliyadi, ndi dziko la Israele, ndiwo Yordani; muyese kuyambira malire a kumpoto kufikira nyanja ya kum'mawa. Ndiyo mbali ya kum'mawa. Ndi mbali ya kumwera kuloza kumwera ndiyo kuyambira ku Tamara kufikira ku madzi a Meribati-Kadesi, ku mtsinje wa Ejipito, ndi ku Nyanja Yaikulu. Ndiyo mbali ya kumwera kuloza kumwera. Ndi mbali ya kumadzulo ndiyo Nyanja Yaikulu, kuyambira malire a kumwera kufikira pandunji polowera ku Hamati. Ndiyo mbali ya kumadzulo. Motero mudzigawire dziko ili monga mwa mafuko a Israele. Ndipo kudzachitika kuti muligawe ndi kuchita maere, likhale cholowa chanu, ndi cha alendo akukhala pakati pa inu; ndipo akhale kwa inu ngati obadwa m'dziko mwa ana a Israele, alandire cholowa pamodzi ndi inu mwa mafuko a Israele. Ndipo kudzatero kuti kufuko kumene mlendo akhalako kumeneko mumpatse cholowa chake, ati Ambuye Yehova. Maina a mafuko tsono ndi awa: Kuyambira nsonga ya kumpoto, ku mbali ya njira ya ku Hetiloni, polowera ku Hamati, Hazara-Enani ku malire a Damasiko kumpoto, ku mbali ya ku Hamati; ndi mbali zake zilinge kum'mawa ndi kumadzulo; Dani akhale nalo gawo limodzi. Ndi m'malire a Dani, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Asere, limodzi. Ndi m'malire a Asere, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Nafutali, limodzi. Ndi m'malire a Nafutali, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Manase, limodzi. Ndi m'malire a Manase, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Efuremu, limodzi. Ndi m'malire a Efuremu, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Rubeni, limodzi. Ndi m'malire a Rubeni, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Yuda, limodzi. Ndi m'malire a Yuda, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo, pakhale chopereka muchipereke, mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu kupingasa kwake, ndi m'litali mwake lilingane ndi magawo enawo, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; ndi malo opatulika akhale pakati pake. Chopereka muchipereke kwa Yehova chikhale cha mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwake, ndi zikwi khumi kupingasa kwake. Ndipo m'mwemo mudzakhala chopereka chopatulika cha ansembe kumpoto, mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwake, ndi kumadzulo mikono zikwi khumi kupingasa kwake, ndi kum'mawa mikono zikwi khumi kupingasa kwake, ndi kumwera mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwake; ndi pakati pake pakhale malo opatulika a Yehova. Chidzakhala cha ansembe opatulidwa a ana a Zadoki, amene anasunga udikiro wanga osasokera, muja anasokera ana a Israele, ndi muja anasokera Alevi. Ndi chiperekocho chikhale chao chotapa pa chopereka cha dziko, ndicho chopatulika kwambiri pa malire a Alevi. Ndipo polingana ndi malire a ansembe Alevi akhale nalo gawo la mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwake, ndi mikono zikwi khumi kupingasa kwake; m'litali mwake monse ndimo mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu, ndi kupingasa kwake mikono zikwi khumi. Ndipo asagulitseko, kapena kulisintha, kapena kupitiriza zipatso zoyamba za dziko; pakuti lili lopatulika la Yehova. Ndipo zikwi zisanu zotsalazo m'kupingasa kwake, chakuno cha mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu, zikhale za ntchito wamba za mudzi, za kumangapo zapabusa; ndi mudzi ukhale pakati pake. Ndi miyeso yake ndi iyi: mbali ya kumpoto, mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu; ndi mbali ya kumwera, mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu; ndi mbali ya kum'mawa, mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu; ndi mbali ya kumadzulo, mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu. Ndipo mudziwo ukhale ndi busa lake; kumpoto mikono mazana awiri mphambu makumi asanu, kumwera mikono mazana awiri mphambu makumi asanu, ndi kum'mawa mikono mazana awiri mphambu makumi asanu, ndi kumadzulo mikono mazana awiri mphambu makumi asanu. Ndipo madera otsalawo m'litali mwake alingane ndi chopereka chopatulika, ndicho mikono zikwi khumi kum'mawa, ndi mikono zikwi khumi kamadzulo, alingane ndi chopereka chopatulika; ndi zipatso zake zikhale za chakudya cha iwo ogwira ntchito m'mudzi. Iwo ogwira ntchito m'mudzi mwa mafuko onse a Israele alimeko. Chopereka chonse ndicho mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwake, mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu kupingasa kwake; muchipereke chopereka chopatulika chaphwamphwa, pamodzi ndi dziko la mudziwo. Ndipo madera ena otsalawo ndiwo a kalonga, mbali ina ndi ina ya chopereka chopatulika ndi ya dziko la mudzi, kutsogolo kwa mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu za chopereka kumalire a kum'mawa, ndi kumadzulo kutsogolo kwa mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu kumalire a kumadzulo, pandunji pa magawo enawo ndiwo cha kalonga; ndipo chopereka chopatulika ndi malo opatulika a Kachisi zidzakhala pakati pake. Kuyambira tsono dziko la Alevi kufikira dziko la mudzi, ndiwo a pakati pa magawo ake a kalonga, pakati pa malire a Yuda ndi malire a Benjamini, kukhale kwa kalonga. Kunena za mafuko otsala tsono, kuyambira kumbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo, Benjamini akhale nalo gawo limodzi. Ndi kumalire a Benjamini, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Simeoni, gawo limodzi. Ndi kumalire a Simeoni kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Isakara, limodzi. Ndi kumalire a Isakara, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Zebuloni, limodzi. Ndi kumalire a Zebuloni, kuyambira kumbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; Gadi, limodzi. Ndi ku malire a Gadi, mbali ya kumwera, kuloza kumwera, malire akhale kuyambira ku Tamara kufikira ku madzi a Meribati-Kadesi, ku mtsinje wa Ejipito, kufikira ku Nyanja Yaikulu. Ili ndi dziko muligawire mafuko a Israele ndi kuchita maere, likhale cholowa chao; ndipo awa ndi magawo ao, ati Ambuye Yehova. Ndipo malekezero a mudzi ndi awa: mbali ya kumpoto ayese mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu; ndi zipata za mudzi zidzakhala monga mwa maina a mafuko a Israele; zipata zitatu kumpoto: chipata chimodzi cha Rubeni, chipata chimodzi cha Yuda, chipata chimodzi cha Levi; ndi ku mbali ya kum'mawa zikwi zinai mphambu mazana asanu, ndi zipata zitatu: chipata chimodzi cha Yosefe, chipata chimodzi cha Benjamini, chipata chimodzi cha Dani; ndi kumbali ya kumwera ayese mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu, ndi zipata zitatu: chipata chimodzi cha Simeoni, chipata chimodzi cha Isakara, chipata chimodzi cha Zebuloni; kumbali ya kumadzulo mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu, ndi zipata zake zitatu: chipata cha Gadi, chipata chimodzi cha Asere, chipata chimodzi cha Nafutali. Pozungulira pake ndipo mikono zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu, ndi dzina la mudziwo kuyambira tsiku ilo lidzakhala, Yehova ali pomwepo. Chaka chachitatu cha Yehoyakimu mfumu ya Yuda, Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adadza ku Yerusalemu, naumangira misasa ya nkhondo. Ndipo Yehova anapereka Yehoyakimu mfumu ya Yuda, m'dzanja lake, pamodzi ndi zipangizo zina za m'nyumba ya Mulungu, namuka nazo iye kudziko la Sinara, kunyumba ya mulungu wake, nalonga zipangizozo m'nyumba ya chuma cha mulungu wake. Ndipo mfumu inauza Asipenazi mkulu wa adindo kuti abwere nao ena a ana a Israele, a mbeu ya mafumu, ndi ya akalonga; anyamata opanda chilema, a maonekedwe okoma, a luso la nzeru zonse, ochenjera m'kudziwa, a luntha lakuganizira, okhoza kuimirira m'chinyumba cha mfumu; ndi kuti awaphunzitse m'mabuku, ndi manenedwe a Ababiloni. Ndipo mfumu inawaikira gawo la chakudya cha mfumu tsiku ndi tsiku, ndi la vinyo wakumwa iye, ndi kuti awalere zaka zitatu, kuti potsiriza pake aimirire pamaso pa mfumu. Mwa awa tsono munali a ana a Yuda, Daniele, Hananiya, Misaele, ndi Azariya. Ndi mkulu wa adindo anawapatsa maina ena; Daniele anamutcha Belitesazara; ndi Hananiya, Sadrake; ndi Misaele, Mesaki; ndi Azariya, Abedenego. Koma Daniele anatsimikiza mtima kuti asadzidetse ndi chakudya cha mfumu, kapena ndi vinyo amamwa; chifukwa chake anapempha mkulu wa adindo amlole asadzidetse. Ndipo Mulungu anamkometsera Daniele mtima wa mkulu wa adindo, amchitire chifundo. Nati mkulu wa adindo kwa Daniele, Ine ndiopa mbuyanga mfumu, amene anakuikirani chakudya chanu ndi chakumwa chanu; pakuti aonerenji nkhope zanu zachisoni zoposa za anyamata olingana ndi inu? Momwemo mudzapalamulitsa mutu wanga kwa mfumu. Nati Daniele kwa kapitao, amene mkulu wa adindo adamuikayo ayang'anire Daniele, Hananiya, Misaele, ndi Azariya, Muyesetu anyamata anu masiku khumi; atipatse zomera m'nthaka tidye, ndi madzi timwe. Pamenepo mupenye maonekedwe athu ndi maonekedwe a anyamata akudya chakudya cha mfumu; ndi monga umo muonera, muchitire anyamata anu. Ndipo anawamvera mau awa, nawayesa masiku khumi. Atatha masiku khumiwo tsono, anaona kuti maonekedwe ao ndi kunenepa kwao anaposa anyamata onse adadyawo zakudya za mfumu. Pamenepo kapitaoyo anachotsa chakudya chao ndi vinyo akadamwa, nawapatsa zomera m'nthaka. Koma anyamata amene anai, Mulungu anawapatsa chidziwitso ndi luntha la m'mabuku ali onse, ndi nzeru; koma Daniele anali nalo luntha la m'masomphenya ndi maloto onse. Atatha masiku inanenawo mfumu kuti alowe nao, mkulu wa adindo analowa nao pamaso pa Nebukadinezara. Ndipo mfumu inalankhula nao, koma mwa iwo onse sanapezeke monga Daniele, Hananiya, Misaele, ndi Azariya; naimirira iwo pamaso pa mfumu. Ndipo m'mau ali onse anzeru ndi aluntha, amene mfumu inawafunsira. Inawapeza akuposa alembi ndi openda onse m'ufumu wake wonse. Nakhala moyo Daniele mpaka chaka choyamba cha mfumu Kirusi. Chaka chachiwiri cha Nebukadinezara mfumu, Nebukadinezarayo analota maloto, ndi mzimu wake unavutika, ndi tulo take tidamwazikira. Pamenepo mfumu inauza munthu aitane alembi, ndi openduza, ndi aula, ndi Ababiloni, amuululire mfumu maloto ake. Nalowa iwo, naimirira pamaso pa mfumu. Niti nao mfumu, Ndalota loto, nuvutika mzimu wanga kudziwa lotolo. Pamenepo Ababiloni anati kwa mfumu m'Chiaramu, Mfumu, mukhale ndi moyo chikhalire: mufotokozere anyamata anu lotoli, ndipo tidzakuuzani kumasulira kwake. Niyankha mfumu, niti kwa Ababiloni, Chandichokera chinthuchi; mukapanda kundidziwitsa lotoli ndi tanthauzo lake, mudzadulidwa nthulinthuli, ndi nyumba zanu zidzayesedwa dzala. Koma mukandidziwitsa lotoli, ndi kumasulira kwake, mudzalandira kwa ine mphatso, ndi mphotho, ndi ulemu waukulu; chifukwa chake mundidziwitse lotoli ndi kumasulira kwake. Nabwerezanso iwo kuyankha, nati, Mfumu ifotokozere anyamata ake lotoli, ndipo tidzaidziwitsa kumasulira kwake. Mfumu inayankha, niti, Ndidziwatu kuti mukunkhuniza dala, pakuona inu kuti chinthuchi chandichokera. Koma mukapanda kundidziwitsa lotoli, mlandu wanu ndi umodzi; popeza mwapanganiranatu mau onama ndi oipa, kuwanena pamaso panga, mpaka idzasanduka nyengo; chifukwa chake mundifotokozere lotoli, momwemo ndidzadziwa kuti mudzandidziwitsa kumasulira kwake komwe. Ababiloni anayankha pamaso pa mfumu, nati, Palibe munthu pa dziko lapansi wokhoza kuwulula mlandu wa mfumu; chifukwa chake palibe mfumu, mkulu, kapena wolamulira, wafunsira chinthu chotere kwa mlembi, kapena wopenduza, kapena Ababiloni ali onse. Pakuti chinthu achifuna mfumu nchapatali; ndipo palibe wina wokhoza kuchiwulula pamaso pa mfumu, koma milungu imene kwao sikuli pamodzi ndi anthu. Chifukwa chake mfumu inakwiya, nizaza kwambiri, nilamulira kuti awaphe anzeru onse m'Babiloni. M'mwemo chilamulirocho chidamveka, ndi eni nzeru adati aphedwe; anafunafunanso Daniele ndi anzake aphedwe. Pamenepo Daniele anabweza mau a uphungu wanzeru kwa Ariyoki mkulu wa olindirira a mfumu, adatulukawo kukapha eni nzeru a ku Babiloni; anayankha nati kwa Ariyoki mkulu wa olindirira a mfumu, Chilamuliro cha mfumu chifulumiriranji? Pamenepo Ariyoki anadziwitsa Daniele chinthuchi. Nalowa Daniele, nafunsa mfumu amuikire nthawi, kuti aululire mfumu kumasulira kwake. Pamenepo Daniele anapita kunyumba kwake, nadziwitsa anzake Hananiya, Misaele, ndi Azariya, chinthuchi; kuti apemphe zachifundo kwa Mulungu wa Kumwamba pa chinsinsi ichi; kuti Daniele ndi anzake asaonongeke pamodzi ndi eni nzeru ena a ku Babiloni. Pamenepo chinsinsicho chinavumbulutsidwa kwa Daniele m'masomphenya a usiku. Ndipo Daniele analemekeza Mulungu wa Kumwamba. Daniele anayankha, nati, Lilemekezedwe dzina la Mulungu kunthawi za nthawi, pakuti nzeru ndi mphamvu zili zake; pakuti amasanduliza nthawi ndi nyengo, achotsa mafumu, nalonga mafumu, apatsa anzeru nzeru, ndi chidziwitso kwa iwo okhoza kuzindikira. Iye avumbulutsa zinthu zakuya ndi zinsinsi; adziwa zokhala mumdima, ndi kuunika kumakhala kwa Iye. Ndikuyamikani ndi kukulemekezani Inu, Mulungu wa makolo anga, pakuti mwandipatsa nzeru ndi mphamvu; ndipo mwandidziwitsa tsopano ichi tachifuna kwa Inu; pakuti mwatidziwitsa mlandu wa mfumu. Potero Daniele analowa kwa Ariyoki amene mfumu idamuika aononge eni nzeru a ku Babiloni; anamuka, natero naye, Usaononga eni nzeru a ku Babiloni, undilowetse kwa mfumu, ndipo ndidzaululira mfumu kumasulirako. Pamenepo Ariyoki analowa naye Daniele kwa mfumu mofulumira; natero nayo, Ndapeza munthu wa ana a ndende a Yuda, ndiye adzadziwitsa mfumu kumasulira kuja. Mfumu inayankha, niti kwa Daniele, amene dzina lake ndiye Belitesazara, Ukhoza kodi kundidziwitsa lotolo ndidalilota, ndi kumasulira kwake? Nayankha Daniele pamaso pa mfumu, nati, Chinsinsi inachitira liuma mfumu, angakhale anzeru, openduza, alembi, kapena alauli, sakhoza kuchiululira mfumu; koma kuli Mulungu Kumwamba wakuvumbulutsa zinsinsi; Iye ndiye wadziwitsa mfumu Nebukadinezara chimene chidzachitika masiku otsiriza. Loto lanu, ndi masomphenya a m'mtima mwanu pakama panu, ndi awa: Inu mfumu, maganizo anu analowa m'mtima mwanu muli pakama panu, akunena za icho chidzachitika m'tsogolomo; ndipo Iye amene avumbulutsa zinsinsi wakudziwitsani chodzachitikacho. Koma ine, chinsinsi ichi sichinavumbulutsidwa kwa ine chifukwa cha nzeru ndili nayo yakuposa wina aliyense wamoyo, koma kuti kumasuliraku kudziwike kwa mfumu, ndi kuti mudziwe maganizo a mtima wanu. Inu mfumu munapenya ndi kuona fano lalikulu. Fanoli linali lalikulu, ndi kunyezimira kwake kunaposa; linali kuima popenyana ndi inu, ndi maonekedwe ake anali oopsa. Fano ili tsono, mutu wake unali wagolide wabwino, chifuwa chake ndi manja ake zasiliva, mimba yake ndi chuuno chake zamkuwa, miyendo yake yachitsulo, mapazi ake mwina chitsulo mwina dongo. Munali chipenyere kufikira mwala unasemedwa popanda manja, umene unagunda fanoli pa mapazi ake okhala chitsulo ndi dongo, nuwaphwanya. Pamenepo chitsulo, dongo, mkuwa, siliva, ndi golide, zinapereka pamodzi, nizinasanduka ngati mungu wa pa madwale a malimwe; ndi mphepo inaziuluza, osapezekanso malo ao; ndi mwala udagunda fanowo unasanduka phiri lalikulu, nudzaza dziko lonse lapansi. Ili ndi loto; kumasulira kwake tsono tikufotokozerani mfumu. Inu mfumu ndinu mfumu ya mafumu, pakuti Mulungu wa Kumwamba anakupatsani ufumu, ndi mphamvu yaikulu, ndi ulemu; ndipo paliponse pokhala ana a anthu Iye anapereka nyama za kuthengo, ndi mbalame za m'mlengalenga, m'dzanja lanu; nakuchititsani ufumu pa izi zonse; inu ndinu mutuwo wagolide. Ndi pambuyo pa inu padzauka ufumu wina wochepa ndi wanu, ndi ufumu wina wachitatu wamkuwa wakuchita ufumu pa dziko lonse lapansi. Ndi ufumu wachinai udzakhala wolimba ngati chitsulo, popeza chitsulo chiphwanya ndi kufoketsa zonse; ndipo monga chitsulo chiswa zonsezi, uwu udzaphwanya ndi kuswa. Ndipo umo mudaonera mapazi ndi zala zake, mwina dongo la woumba, mwina chitsulo; ufumuwo udzakhala wogawanika, koma momwemo mudzakhala mphamvu ya chitsulo; popeza mudaona chitsulo chosanganizika ndi dongo. Ndi zala za mapazi, mwina chitsulo ndi mwina dongo, momwemo ufumuwo, mwina wolimba mwina wogamphuka. Ndi umo mudaonera chitsulo chosanganizika ndi dongo, iwo adzadzisokoneza ndi ana a anthu wamba; koma sadzaphatikizana, monga umo chitsulo sichimasanganizikana ndi dongo. Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzaonongeka kunthawi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu ao onse, nudzakhala chikhalire. Umo mudaonera kuti mwala unasemedwa m'phiri popanda manja, ndi kuti udapera chitsulo, mkuwa, dongo, siliva, ndi golide; Mulungu wamkulu wadziwitsa mfumu chidzachitika m'tsogolomo; lotoli nloona, ndi kumasulira kwake kwakhazikika. Pamenepo mfumu Nebukadinezara anagwa nkhope yake pansi, nalambira Daniele, nati amthirire nsembe yaufa ndi ya zonunkhira zokoma. Mfumu inamyankha Daniele, niti, Zoona Mulungu wako ndiye Mulungu wa milungu, ndi Mbuye wa mafumu, ndi wovumbulutsa zinsinsi; popeza wakhoza kuvumbulutsa chinsinsi ichi. Pamenepo mfumu inasandutsa Daniele wamkulu, nimpatsa mphatso zazikulu zambiri, namlamuliritsa dera lonse la ku Babiloni; nakhala iye kazembe wamkulu wa anzeru onse a ku Babiloni. Pamenepo Daniele anapempha mfumu, ndipo anaika Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, ayang'anire ntchito za dera la ku Babiloni. Koma Daniele anakhala m'bwalo la mfumu. Mfumu Nebukadinezara anapanga fano lagolide, msinkhu wake mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi thunthu lake mikono isanu ndi umodzi; analiimika pa chidikha cha Dura, m'dera la ku Babiloni. Ndipo mfumu Nebukadinezara inatumiza kukasonkhanitsa akalonga, akazembe, ndi ziwanga, oweruza, akulu osunga chuma, mandoda, ankhoswe, ndi olamulira onse a madera, abwera kuzulula fanoli adaliimika mfumu Nebukadinezara. Pamenepo akalonga, akazembe, ndi ziwanga, oweruza, akulu osunga chuma, mandoda, ankhoswe, ndi olamulira onse a madera, anasonkhanira kupereka fano adaliimika mfumu Nebukadinezara, naimirira pamaso pa fano adaliimika Nebukadinezara. Ndipo wolalikira anafuulitsa, kuti, Akulamulirani inu anthu, mitundu ya anthu a manenedwe osiyana, kuti pakumva inu mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ngoli, ndi zoimbitsa zilizonse, mugwadire ndi kulambira fano lagolide adaliimika mfumu Nebukadinezara; ndipo aliyense wosagwadira ndi kulambira, adzaponyedwa nthawi yomweyo m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto. Potero nthawi yomweyo pakumva anthu onse mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ndi zoimbitsa zilizonse, anthu onse, mitundu ya anthu a manenedwe osiyana, anagwadira, nalambira fano lagolide adaliimika mfumu Nebukadinezara. Chifukwa chake anayandikira Ababiloni ena nthawi yomweyi, naneneza Ayuda. Anayankha, nati kwa mfumu Nebukadinezara, Mfumu, mukhale ndi moyo chikhalire. Inu mfumu mwalamulira kuti munthu aliyense amene adzamva mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ngoli, ndi zoimbitsa zilizonse, agwadire, nalambire fanolo lagolide; ndi yense wosagwadira ndi kulambira adzaponyedwa m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto. Alipo Ayuda amene munawaika ayang'anire ntchito ya dera la ku Babiloni, Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, amuna awa, mfumu, sanasamalire inu, satumikira milungu yanu, kapena kulambira fano lagolide mudaliimikalo. Pamenepo Nebukadinezara, mumkwiyo ndi m'ukali wake, anawauza abwere nao Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego. Ndipo anabwera nao amunawa kwa mfumu. Nebukadinezara anayankha, nati kwa iwo, Kodi mutero dala, Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, kusatumikira milungu yanga, ndi kusalambira fano lagolide ndinaliimikalo? Mukavomereza tsono, pakumva mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ndi ngoli, ndi zoimbitsa zilizonse, kugwadira ndi kulambira fano ndinalipanga, chabwino; koma mukapanda kulambira, mudzaponyedwa nthawi yomweyi m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto; ndipo mulungu amene adzakulanditsani m'manja mwanga ndani? Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, anayankha, nati kwa mfumu Nebukadinezara, Sikufunika kuti tikuyankheni pa mlandu uwu. Taonani, Mulungu wathu amene timtumikira akhoza kutilanditsa m'ng'anjo yotentha yamoto, nadzatilanditsa m'dzanja lanu, mfumu. Koma akapanda kutero, dziwani, mfumu, kuti sitidzatumikira milungu yanu, kapena kulambira fano lagolide mudaliimikalo. Pamenepo Nebukadinezara anadzazidwa ndi ukali, ndi maonekedwe a nkhope yake anansandulikira Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego; anayankha, nati asonkheze ng'anjo kasanu ndi kawiri koposa umo amasonkhezera. Nauza amuna ena amphamvu a m'khamu lake la nkhondo amange Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, ndi kuwaponya m'ng'anjo yotentha yamoto. Pamenepo amuna awa anamangidwa ali chivalire zofunda zao, malaya ao, ndi nduwira zao, ndi zovala zao zina; naponyedwa m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto. Motero, popeza mau a mfumu anafulumiza, ndi ng'anjo inatentha koposa, lawi la moto linapha iwo aja ananyamula Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego. Ndipo amuna atatu awa, Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, anagwa pansi omangidwa m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto. Pamenepo mfumu Nebukadinezara anadabwa, nauka msanga, nanena nati kwa mandoda ake, Kodi sitinaponya amuna atatu omangidwa m'kati mwa moto? Anayankha nati kwa mfumu, Inde mfumu. Anayankha, nati, Taonani, ndilikuona amuna anai omasuka, alikuyenda m'kati mwa moto; ndipo alibe kuphwetekwa, ndi maonekedwe a wachinai akunga mwana wa milungu. Pamenepo Nebukadinezara anayandikira pa khomo la ng'anjo yotentha yamoto, analankhula, nati, Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, inu atumiki a Mulungu Wam'mwambamwamba, tulukani, idzani kuno. Pamenepo Sadrake, Mesake, ndi Abedenego, anatuluka m'kati mwa moto. Ndipo akalonga, akazembe, ndi ziwanga, ndi mandoda a mfumu, atasonkhana, anaona amuna awa, kuti moto unalibe mphamvu pa matupi ao, losawauka tsitsi la pamutu pao, ndi zofunda zao zosasandulika, fungo lomwe lamoto losawaomba. Nebukadinezara ananena, nati, Alemekezedwe Mulungu wa Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, amene anatuma mthenga wake, napulumutsa atumiki ake omkhulupirira Iye, nasanduliza mau a ine mfumu, napereka matupi ao kuti asatumikire kapena kulambira mulungu wina yense, koma Mulungu waowao. Chifukwa chake ndilamulira kuti anthu ali onse, mtundu uliwonse, ndi a manenedwe ali onse, akunenera molakwira Mulungu wa Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, adzadulidwa nthulinthuli, ndi nyumba zao zidzasanduka dzala; popeza palibe mulungu wina akhoza kulanditsa motero. Pamenepo mfumu inakuza Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, m'dera la ku Babiloni. Mfumu Nebukadinezara, kwa anthu mitundu ya anthu, ndi a manenedwe okhala pa dziko lonse lapansi: Mtendere uchulukire inu. Chandikomera kuonetsa zizindikiro ndi zozizwa, zimene anandichitira Mulungu Wam'mwambamwamba. Ha! Zizindikiro zake nzazikulu, ndi zozizwa zake nza mphamvu, ufumu wake ndiwo ufumu wosatha, ndi kulamulira kwake ku mibadwomibadwo. Ine Nebukadinezara ndinalimkupumula m'nyumba mwanga, ndi kukhala mwaufulu m'chinyumba changa. Ndinaona loto lakundiopsa, ndi zolingirira za pakama panga, ndi masomphenya a m'mtima mwanga, zinandivuta ine. Chifukwa chake ndinalamulira kuti adze kwa ine anzeru onse a ku Babiloni, kuti andidziwitse kumasulira kwake kwa lotoli. Pamenepo anafika alembi, openda, Ababiloni, ndi alauli; ndipo ndinawafotokozera lotoli, koma sanandidziwitse kumasulira kwake. Koma potsiriza pake analowa pamaso panga Daniele, dzina lake ndiye Belitesazara, monga mwa dzina la mulungu wanga, amenenso muli mzimu wa milungu yoyera m'mtima mwake; ndipo ndinamfotokozera lotoli pamaso pake, ndi kuti, Belitesazara iwe, mkulu wa alembi, popeza ndidziwa kuti mwa iwe muli mzimu wa milungu yoyera, ndi kuti palibe chinsinsi chikusautsa, undifotokozere masomphenya a loto langa ndalotali, ndi kumasulira kwake. Masomphenya a m'mtima mwanga pakama panga ndi awa: Ndinapenya ndi kuona mtengo pakati pa dziko lapansi, msinkhu wake ndi waukulu. Mtengowo unakula, nulimba, ndi msinkhu wake unafikira kumwamba, nuonekera mpaka chilekezero cha dziko lonse lapansi. Masamba ake anali okoma, ndi zipatso zake zinachuluka, ndi m'menemo munali zakudya zofikira onse, nyama za kuthengo zinatsata mthunzi wake, ndi mbalame za m'mlengalenga zinafatsa m'thambi zake, ndi nyama zonse zinadyako. Ndinaona m'masomphenya a m'mtima mwanga pakama panga, taonani, mthenga woyera anatsika kumwamba. Anafuulitsa, natero, Likhani mtengowo, sadzani nthambi zake, yoyolani masamba ake, mwazani zipatso zake, nyama za kuthengo zichoke pansi pake, ndi mbalame pa nthambi zake. Koma siyani chitsa ndi mizu yake m'nthaka, chomangidwa ndi mkombero wa chitsulo ndi mkuwa, mu msipu wa kuthengo; nchokhathamira ndi mame a kumwamba, ndi gawo lake likhale pamodzi ndi nyama zili m'machire a m'dziko. Mtima wake usandulike, usakhalenso mtima wa munthu, apatsidwe mtima wonga wa nyama, nizimpitire nthawi zisanu ndi ziwiri. Chitsutso ichi adachilamulira amithenga oyerawo, anachifunsa, nachinena, kuti amoyo adziwe kuti Wam'mwambamwamba alamulira m'ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna, nauutsira wolubukira anthu. Loto ili ndinaliona ine mfumu Nebukadinezara; ndipo iwe, Belitesazara, undifotokozere kumasulira kwake, popeza anzeru onse a m'ufumu wanga sakhoza kundidziwitsa kumasulira kwake; koma iwe ukhoza, popeza mwa iwe muli mzimu wa milungu yoyera. Pamenepo Daniele, dzina lake ndiye Belitesazara anadabwa nthawi, namsautsa maganizo ake. Mfumu inayankha, niti, Belitesazara, lisakusautse lotoli, kapena kumasulira kwake. Belitesazara anayankha, nati, Mbuye wanga, lotoli likadakhala la iwo akudana nanu, ndi kumasulira kwake kwa iwo akuutsana nanu. Mtengo mudauona umene unakula, nukhala wolimba, nufikira kumwamba msinkhu wake, nuonekera pa dziko lonse lapansi, umene masamba ake anali okoma, ndi zipatso zake zochuluka, ndi m'menemo munali chakudya chofikira onse, umene nyama za kuthengo zinakhala pansi pake, ndi mbalame za m'mlengalenga zinapeza pokhala pao pa nthambi yake; ndinu, mfumu; mwakula, mwalimba, pakuti ukulu wanu wakula, nufikira kumwamba, ndi ufumu wanu ku chilekezero cha dziko lapansi. Tsono, kuti mfumu inaona mthenga woyera wotsika kumwamba, ndi kuti, Likhani mtengowo ndi kuuononga, koma siyani chitsa chake ndi mizu m'nthaka, chomangidwa ndi mkombero wa chitsulo ndi mkuwa, mu msipu wa kuthengo, nichikhale chokhathamira ndi mame a kumwamba, ndi gawo lake likhale pamodzi ndi nyama za kuthengo, mpaka zitampitira nthawi zisanu ndi ziwiri; kumasulira kwake ndi uku, mfumu; ndipo chilamuliro cha Wam'mwambamwamba chadzera mbuye wanga mfumu: kuti adzakuingitsani kukuchotsani kwa anthu, ndi pokhala panu padzakhala pamodzi ndi nyama za kuthengo; ndipo mudzadya udzu ngati ng'ombe, nimudzakhala wokhathamira ndi mame a kumwamba, nizidzakupitirani nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka mudzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira m'ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna mwini. Ndipo kuti anauza asiye chitsa ndi mizu ya mtengo, ufumu wanu udzakhazikikira inu, mukakatha kudziwa kuti Kumwamba kumalamulira. Chifukwa chake, mfumu, kupangira kwanga kukomere inu, dulani machimo anu ndi kuchita chilungamo, ndi mphulupulu zanu mwa kuchitira aumphawi chifundo; kuti kapena nthawi ya mtendere wanu italike. Chonsechi chinagwera mfumu Nebukadinezara. Itatha miyezi khumi ndi iwiri, analikuyenda m'chinyumba chachifumu cha ku Babiloni. Mfumu inanena, niti, Suyu Babiloni wamkulu ndinammanga, akhale pokhala pachifumu, ndi mphamvu yanga yaikulu uoneke ulemerero wa chifumu changa? Akali m'kamwa mwa mfumu mau awa, anamgwera mau ochokera kumwamba, ndi kuti, Mfumu Nebukadinezara, anena kwa iwe: ufumu wakuchokera. Nadzakuinga kukuchotsa kwa anthu, ndi pokhala pako udzakhala pamodzi ndi nyama za kuthengo; adzakudyetsa udzu ngati ng'ombe; nizidzakupitira nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka udzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira m'ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna mwini. Nthawi yomweyo anachitika mau awa kwa Nebukadinezara; anamuinga kumchotsa kwa anthu; nadya udzu ngati ng'ombe iye, ndi thupi lake linakhathamira ndi mame a kumwamba, mpaka tsitsi lake lidamera ngati nthenga za chiombankhanga ndi makadabo ake ngati makadabo a mbalame. Atatha masiku awa tsono, ine Nebukadinezara ndinakweza maso anga kumwamba, ndi nzeru zanga zinandibwerera; ndipo ndinalemekeza Wam'mwambamwamba, ndi kumyamika ndi kumchitira ulemu Iye wokhala chikhalire; pakuti kulamulira kwake ndiko kulamulira kosatha, ndi ufumu wake ku mibadwomibadwo; ndi okhala pa dziko lapansi onse ayesedwa achabe; ndipo Iye achita mwa chifuniro chake m'khamu la kumwamba ndi mwa okhala pa dziko lapansi; ndipo palibe woletsa dzanja lake, kapena wakunena naye, Muchitanji? Nthawi yomweyi nzeru zanga zinandibwerera, ndi chifumu changa ndi kunyezimira kwanga zinandibwerera, kuti uonekenso ulemerero wa ufumu wanga; ndi mandoda anga ndi akulu anga anandifuna; ndipo ndinakhazikika m'ufumu wanga, Iye nandionjezeranso ukulu wochuluka. Tsono ine Nebukadinezara ndiyamika, ndi kukuza, ndi kulemekeza Mfumu ya Kumwamba, pakuti ntchito zake zonse nzoona, ndi njira zake chiweruzo; ndi oyenda m'kudzikuza kwao, Iye akhoza kuwachepetsa. Mfumu Belisazara anakonzera anthu ake akulu chikwi chimodzi madyerero akulu, namwa vinyo pamaso pa chikwicho. Belisazara, pakulawa vinyo, anati abwere nazo zotengera za golide ndi siliva adazichotsa Nebukadinezara atate wake ku Kachisi ali ku Yerusalemu, kuti mfumu ndi akulu ake, akazi ake ndi akazi ake ang'ono, amweremo. Nabwera nazo zotengera zagolide adazichotsa ku Kachisi wa nyumba ya Mulungu ya ku Yerusalemu, ndipo mfumu ndi akulu ake, akazi ake ndi akazi ake ang'ono, anamweramo. Anamwa vinyo, nalemekeza milungu yagolide, ndi yasiliva, yamkuwa, yachitsulo, yamtengo, ndi yamwala. Nthawi yomweyo zinabuka zala za dzanja la munthu, nizinalemba pandunji pa choikapo nyali, pomata pa khoma la chinyumba cha mfumu; ndipo mfumu inaona nsonga yake ya dzanja lidalembalo. Pamenepo padasandulika pa nkhope pake pa mfumu, ndi maganizo ake anamsautsa, ndi mfundo za m'chuuno mwake zinaguluka, ndi maondo ake anaombana. Nifuulitsa mfumu abwere nao openda, Ababiloni, ndi alauli. Mfumu inalankhula, niti kwa anzeru a ku Babiloni, Aliyense amene adzawerenga lemba ili, nadzandifotokozera kumasulira kwake, adzavekedwa chibakuwa, ndi unyolo wagolide m'khosi mwake, nadzakhala wolamulira wachitatu m'ufumuwu. Pamenepo analowa anzeru onse a mfumu, koma sanakhoze kuwerenga lembalo, kapena kudziwitsa mfumu kumasulira kwake. Ndipo mfumu Belisazara anavutika kwambiri, ndi nkhope yake inasandulika, ndi akulu ake anathedwa nzeru. Chifukwa cha mau a mfumu ndi akulu ake mkazi wamkulu wa mfumu analowa m'nyumba ya madyerero; mkazi wa mfumu ananena, nati, Mfumu, mukhale ndi moyo kosatha; asakuvuteni maganizo anu, ndi nkhope yanu isasandulike; pali munthu m'ufumu mwanu mwa iye muli mzimu wa milungu yoyera; ndipo masiku a atate wanu munapezeka mwa iye kuunika, ndi luntha, ndi nzeru, ngati nzeru ya milungu; ndipo mfumu Nebukadinezara atate wanu, inde mfumu atate wanu anamuika akhale mkulu wa alembi, openda, Ababiloni, ndi alauli; popeza m'Daniele yemweyo, amene mfumu adamutcha Belitesazara, mudapezeka mzimu wopambana, ndi chidziwitso, ndi luntha, kumasulira maloto ndi kutanthauzira mau ophiphiritsa ndi kumasula mfundo. Amuitane Daniele tsono, iye adzafotokozera kumasuliraku. Pamenepo analowa naye Daniele kwa mfumu. Mfumu inayankha, niti kwa Daniele, Ndiwe kodi Daniele uja wa ana a ndende a Yuda, amene mfumu atate wanga anatenga ku Yuda? Ndamva za iwe kuti muli mzimu wa milungu mwa iwe, ndi kuti mupezeka mwa iwe kuunika, ndi luntha, ndi nzeru zopambana. Ndipo tsono anabwera nao kwa ine anzeru, openda, kuti awerenge lemba ilo, ndi kundidziwitsa kumasulira kwake; koma sanakhoze kufotokozera kumasulira kwa chinthuchi. Koma ndamva ine za iwe, kuti ukhoza kutanthauzira mau, ndi kumasula mfundo; tsono ukakhoza kuwerenga lembalo, ndi kundidziwitsa kumasulira kwake, udzavekedwa chibakuwa, ndi unyolo wagolide m'khosi mwako; nudzakhala wolamulira wachitatu m'ufumuwo. Pamenepo anayankha Daniele, nati kwa mfumu, Mphatso zanu zikhale zanu, ndi mphotho zanu mupatse wina; koma ndidzawerengera mfumu lembalo, ndi kumdziwitsa kumasulira kwake. Mfumu inu, Mulungu Wam'mwambamwamba anapatsa Nebukadinezara atate wanu ufumuwu, ndi ukulu, ndi ulemerero, ndi chifumu; ndipo chifukwa cha ukulu adampatsawo anthu onse, mitundu yonse ya anthu, amanenedwe onse, ananjenjemera, naopa pamaso pake; amene anafuna kuwapha anawapha; amene anafuna kuwasunga anawasunga amoyo; amene anafuna kuwakweza anawakweza; amene anafuna kuwatsitsa anawatsitsa. Koma pokwezeka mtima wake, nulimba mzimu wake kuchita modzikuza, anamtsitsa pa mpando wa ufumu wake, namchotsera ulemerero wake; ndipo anamuinga kumchotsa kwa ana a anthu, ndi mtima wake unasandulika ngati wa nyama za kuthengo, ndi pokhala pake mpa mbidzi, anamdyetsa udzu ngati ng'ombe, ndi thupi lake linakhathamira ndi mame a kumwamba; mpaka anadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira m'ufumu wa anthu, nauikira aliyense Iye afuna mwini. Ndipo inu mwana wake, Belisazara inu, simunadzichepetsa m'mtima mwanu, chinkana munazidziwa izi zonse; koma munadzikweza kutsutsana naye Ambuye wa Kumwamba; ndipo anabwera nazo zotengera za nyumba yake kwa inu; ndi inu ndi akulu anu, akazi anu ndi akazi anu ang'ono, mwamweramo vinyo; mwalemekezanso milungu yasiliva, ndi yagolide, yamkuwa, yachitsulo, yamtengo, ndi yamwala, imene siiona kapena kumva, kapena kudziwa; ndi Mulungu amene m'dzanja mwake muli mpweya wanu, ndi njira zanu zonse, yemweyo simunamchitira ulemu. Pamenepo nsonga ya dzanja inatumidwa kuchokera pamaso pake, nililembedwa lembali. Ndipo lemba lolembedwa ndi ili: MENE MENE TEKEL UFARSIN. Kumasulira kwake kwa mau awa ndi uku: MENE, Mulungu anawerenga ufumu wanu, nautha. TEKEL, Mwayesedwa pamiyeso, nimupezeka mwaperewera. PERES, ufumu wanu wagawika, nuperekedwa kwa Amedi ndi Aperisi. Pamenepo Belisazara analamulira, ndipo anaveka Daniele chibakuwa, ndi unyolo wagolide m'khosi mwake, nalalikira za iye kuti ndiye wolamulira wachitatu m'ufumumo. Usiku womwewo Belisazara mfumu ya Ababiloni anaphedwa. Ndipo Dariusi Mmedi analandira ufumuwo ali wa zaka makumi asanu ndi limodzi mphambu ziwiri. Kudamkomera Dariusi kuikira ufumuwo akalonga zana limodzi mphambu makumi awiri akhale m'madera onse a ufumu; ndi akuyang'anira iwo akulu atatu, woyamba wao ndi Daniele; kuti akalonga awa adziwerengere kwa iwo, ndi kuti za mfumu zisasoweke. Pamenepo Daniele amene anaposa akuluwa ndi akalonga, popeza munali mzimu wopambana mwa iye, ndi mfumu inati imuike woyang'anira ufumu wonse. Ndipo akuluwa ndi akalonga anayesa kumtola chifukwa Daniele, kunena za ufumuwo; koma sanakhoze kupeza chifukwa kapena cholakwira, popeza anali wokhulupirika; ndipo saonana chosasamala kapena cholakwa chilichonse mwa iye. Pamenepo anthu awa anati, Sitidzamtola chifukwa chilichonse Daniele amene, tikapanda kumtola ichi pa chilamulo cha Mulungu wake. Ndipo akulu awa ndi akalonga anasonkhana kwa mfumu mofulumira, natero nayo, Mfumu Dariusi, mukhale ndi moyo chikhalire. Akulu onse a ufumuwo, ndi akazembe ndi akalonga, mandoda, ndi ziwanga, anapangana kukhazika lemba lachifumu, ndi kuikapo choletsa cholimba, kuti aliyense akapempha kanthu kwa mulungu aliyense, kapena kwa munthu aliyense masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m'dzenje la mikango. Tsopano, mfumu, mukhazikitse choletsacho, ndi kutsimikiza cholembedwacho, kuti chisasinthike monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperisi, amene sasinthika. Momwemo mfumu Dariusi anatsimikiza cholembedwa ndi choletsacho. Ndipo podziwa Daniele kuti adatsimikiza cholembedwacho, analowa m'nyumba mwake, m'chipinda mwake, chimene mazenera ake anatseguka oloza ku Yerusalemu; ndipo anagwada maondo ake tsiku limodzi katatu, napemphera, navomereza pamaso pa Mulungu wake monga umo amachitira kale lonse. Pamenepo anasonkhana anthu awa, napeza Daniele alikupemphera ndi kupembedza pamaso pa Mulungu wake. Ndipo anayandikira, nanena pamaso pa mfumu za choletsacho cha mfumu, Kodi simunatsimikiza choletsacho, kuti aliyense akapempha kanthu kwa mulungu aliyense, kapena kwa munthu aliyense, masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m'dzenje la mikango? Mfumu niyankha, niti, Choona chinthuchi, monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperisi amene sasinthika. Pamenepo anayankha, nati pamaso pa mfumu, Daniele uja wa ana a ndende a Yuda sasamalira inu, mfumu, kapena choletsa munachitsimikizacho; koma apempha pemphero lake katatu tsiku limodzi. Ndipo mfumu m'mene atamva mau awa anaipidwa kwambiri, naika mtima wake pa Daniele kuti amlanditse, nayesetsa mpaka polowa dzuwa kumlanditsa. Koma anthu awa anasonkhana kwa mfumu, nati kwa mfumu, Dziwani, mfumu, kuti lamulo la Amedi ndi Aperisi, ndilo kuti choletsa chilichonse ndi lemba lililonse idazikhazikira mfumu, zisasinthike. Pamenepo inalamula mfumu, ndipo anadza naye Daniele, namponya m'dzenje la mikango. Ndipo mfumu inalankhula, niti kwa Daniele, Mulungu wako amene umtumikira kosalekeza, Iyeyu adzakulanditsa. Ndipo anatenga mwala, nauika pakamwa pa dzenje, niukomera mfumu ndi chosindikizira chake, ndi chosindikizira cha akulu ake, kuti kasasinthike kanthu ka Daniele. Pamenepo mfumu inamuka kuchinyumba chake, nichezera kusala usikuwo, ngakhale zoimbitsa sanabwere nazo pamaso pake, ndi m'maso mwake munamuumira. Nilawira mamawa mfumu, nimuka mofulumira kudzenje la mikango. Ndipo poyandikira padzenje inafuula ndi mau achisoni mfumu, ninena, niti kwa Daniele, Daniele, mnyamata wa Mulungu wamoyo, kodi Mulungu wako, amene umtumikira kosalekeza, wakhoza kukulanditsa kwa mikango? Pamenepo Daniele anati kwa mfumu, Mfumu, mukhale ndi moyo chikhalire. Mulungu wanga watuma mthenga wake, natseka pakamwa pa mikango; ndipo siinandipweteka, chifukwa anandiona wosachimwa pamaso pake, pamaso panunso, mfumu, sindinalakwa. Pamenepo mfumu inakondwera kwambiri, niwauza atulutse Daniele m'dzenje. Momwemo anamtulutsa Daniele m'dzenje, ndi pathupi pake sipadaoneka bala, popeza anakhulupirira Mulungu wake. Ndipo italamulira mfumu, anabwera nao amuna aja adamneneza Daniele, nawaponya m'dzenje la mikango, iwowa, ana ao, ndi akazi ao; ndipo asanafike pansi pa dzenje mikango inawaposa mphamvu, niphwanya mafupa ao onse. Pamenepo mfumu Dariusi analembera kwa anthu, mitundu ya anthu, ndi a manenedwe onse okhala pa dziko lonse lapansi, Mtendere uchulukire inu. Ndilamulira ine kuti m'maiko onse a ufumu wanga anthu anjenjemere, naope pamaso pa Mulungu wa Daniele; pakuti Iye ndiye Mulungu wamoyo wakukhala chikhalire, ndi ufumu wake ngwosaonongeka, ndi kulamulira kwake kudzakhala mpaka chimaliziro. Iye apulumutsa, nalanditsa, nachita zizindikiro ndi zozizwa m'mwamba ndi pa dziko lapansi, ndiye amene anapulumutsa Daniele kumphamvu ya mikango. Momwemo Daniele amene anakuzikabe pokhala Dariusi mfumu, ndi pokhala mfumu Kirusi wa ku Persiya. Chaka choyamba cha Belisazara mfumu ya ku Babiloni Daniele anaona loto, naona masomphenya a m'mtima mwake pakama pake; ndipo analemba lotolo, nalifotokozera, mwachidule. Daniele ananena, nati, Ndinaona m'masomphenya anga usiku, taonani, mphepo zinai za mumlengalenga zinabuka pa nyanja yaikulu. Ndipo zinatuluka m'nyanja zilombo zazikulu zinai zosiyanasiyana. Choyamba chinanga mkango, chinali nao mapiko a chiombankhanga, ndinapenyera mpaka nthenga zake zinathothoka, nichinakwezeka kudziko, ndi kuimitsidwa ndi mapazi awiri ngati munthu, nichinapatsidwa mtima wa munthu. Ndipo taonani, chilombo china chachiwiri chikunga chimbalangondo chinatundumuka mbali imodzi; ndi m'kamwa mwake munali nthiti zitatu pakati pa mano ake; ndipo anatero nacho, Nyamuka, lusira nyama zambiri. Pambuyo pake ndinapenya ndi kuona china ngati nyalugwe, chinali nao mapiko anai a nkhuku pamsana pake, chilombocho chinali nayonso mitu inai, nichinapatsidwa ulamuliro. Pambuyo pake ndinaona m'masomphenya a usiku, ndi kuona chilombo chachinai, choopsa ndi chochititsa mantha, ndi champhamvu choposa, chinali nao mano akulu achitsulo, chinalusa ndi kuphwanya ndi kupondereza chotsala ndi mapazi ake; chinasiyana ndi zilombo zonse zidachitsogolera; ndipo chinali ndi nyanga khumi. Ndinali kulingilirira za nyangazi, taonani, pakati pa izo panaphuka nyanga ina, ndiyo yaing'ono; patsogolo pake zitatu za nyanga zoyambazi zinazulidwa ndi mizu yomwe; ndipo taonani, m'nyanga m'menemo munali maso ngati maso a munthu, ndi pakamwa palikunena zazikulu. Ndinapenyerera mpaka anaikapo mipando yachifumu, nikhalapo Nkhalamba ya kale lomwe, zovala zake zinali za mbu ngati chipale chofewa, ndi tsitsi la pa mutu pake ngati ubweya woyera, mpando wachifumu unali malawi amoto, ndi njinga zake moto woyaka. Mtsinje wamoto unayenda wotuluka pamaso pake, zikwizikwi anamtumikira, ndi unyinji wosawerengeka unaima pamaso pake, woweruza mlandu anakhalapo, ndi mabuku anatsegulidwa. Pamenepo ndinapenyera chifukwa cha phokoso la mau akulu idanena nyangayi; ndinapenyera mpaka adachipha chilombochi, ndi kuononga mtembo wake, ndi kuupereka utenthedwe ndi moto. Ndipo zilombo zotsalazo anazichotsera ulamuliro wao, koma anatalikitsa moyo wao, ukhalenso nyengo ndi nthawi. Ndinaona m'masomphenya a usiku, taonani, anadza ndi mitambo ya kumwamba wina ngati mwana wa munthu, nafika kwa Nkhalamba ya kale lomwe; ndipo anamyandikizitsa pamaso pake. Ndipo anampatsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, amtumikire; ulamuliro wake ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wake sudzaonongeka. Koma ine Daniele, mzimu wanga unalaswa m'kati mwa thupi langa, ndi masomphenya a m'mtima mwanga anandivuta. Ndinayandikira kwa wina wa iwo akuimako ndi kumfunsa za choonadi za ichi chonse. Ndipo ananena nane, nandidziwitsa kumasulira kwake kwa zinthuzi: Zilombo zazikulu izi zinai ndizo mafumu anai amene adzauka pa dziko lapansi. Koma opatulika a Wam'mwambamwamba adzalandira ufumuwo, ndi kukhala nao ufumu kosatha, kunthawi zonka muyaya. Pamenepo ndinafuna kudziwa choonadi cha chilombo chachinai chija chidasiyana nazo zonsezi, choopsa chopambana, mano ake achitsulo, ndi makadabo ake amkuwa, chimene chidalusa, ndi kuphwanya, ndi kupondereza zotsala ndi mapazi ake; ndi za nyanga khumi zinali pamutu pake, ndi nyanga ina idaphukayi, imene zidagwa zitatu patsogolo pake; nyangayo idali ndi maso ndi pakamwa pakunena zazikulu, imene maonekedwe ake anaposa zinzake. Ndinapenya, ndipo nyanga yomweyi inachita nkhondo ndi opatulikawo, niwalaka, mpaka inadza Nkhalamba ya kale lomwe; ndi mlandu unakomera opatulika a Wam'mwambamwamba, nifika nthawi yakuti ufumu unali wao wa opatulikawo. Anatero, chilombo chachinai ndicho ufumu wachinai pa dziko lapansi, umene udzasiyana nao maufumu onse, nudzalusira dziko lonse lapansi, nudzalipondereza ndi kuliphwanya. Kunena za nyanga khumi, m'ufumu uwu adzauka mafumu khumi, ndi pambuyo pao idzauka ina; iyo idzasiyana ndi oyamba aja, nidzachepetsa mafumu atatu. Nidzanena mau akutsutsana ndi Wam'mwambamwamba, nidzalemetsa opatulika a Wam'mwambamwamba, nidzayesa kusintha nthawizo ndi chilamulo; ndipo adzaperekedwa m'dzanja lake mpaka nthawi imodzi, ndi nthawi zina, ndi nthawi yanusu. Koma woweruza mlandu adzakhalako, ndipo adzachotsa ulamuliro wake, kuutha ndi kuuononga kufikira chimaliziro. Ndipo ufumu, ndi ulamuliro, ndi ukulu wa maufumu, pansi pa thambo lonse, zidzapatsidwa kwa anthu a opatulika a Wam'mwambamwamba; ufumu wake ndiwo ufumu wosatha, ndi maiko onse adzamtumikira ndi kummvera. Kutha kwake kwa chinthuchi nkuno. Ine Daniele, maganizo anga anandivuta kwambiri, ndi nkhope yanga inasandulika; koma ndinasunga chinthuchi m'mtima mwanga. Chaka chachitatu cha Belisazara mfumu masomphenya anandionekera kwa ine Daniele, atatha kundionekera oyamba aja. Ndipo ndinaona m'masomphenya; tsono kunali, pakuwaona ine ndinali m'Susa, m'nyumba ya mfumu, ndiwo m'dziko la Elamu; ndinaona m'masomphenya kuti ndinali kumtsinje Ulai. Ndipo ndinakweza maso anga ndi kupenya; taonani, panaima pamtsinje nkhosa yamphongo yokhala nazo nyanga ziwiri, ndi nyanga ziwirizo zinali za msinkhu wautali, koma imodzi inaposa inzake; yoposayo inaphuka m'mbuyo. Ndinaona nkhosa yamphongo ilikugunda kumadzulo, ndi kumpoto, ndi kumwera; ndipo panalibe zamoyo zokhoza kuima pamaso pake; panalibenso wakulanditsa m'dzanja lake; koma inachita monga mwa chifuniro chake, nidzikulitsa. Ndipo polingirirapo ine, taonani, wadza tonde wochokera kumadzulo, pa nkhope ya dziko lonse lapansi, wosakhudza nthaka; ndi mbuziyo inali ndi nyanga yooneka bwino pakati pa maso ake. Ndipo anadzera nkhosa yamphongoyo yokhala ndi nyanga ziwiri, imene ndidaiona ilikuima kumtsinje, naithamangira ndi mphamvu yake yaukali. Ndipo ndinamuona wayandikira pafupi pa nkhosa yamphongo, nawawidwa mtima nayo, naigunda nkhosa yamphongo, nathyola nyanga zake ziwiri; ndipo mphongoyo inalibe mphamvu yakuima pamaso pake, koma anaigwetsa pansi, naipondereza; ndipo panalibe wakupulumutsa mphongoyo m'dzanja lake. Ndipo tondeyo anadzikulitsa kwakukulu, koma atakhala wamphamvu, nyanga yake yaikulu inathyoka; ndi m'malo mwake munaphuka nyanga zinai zooneka bwino, zoloza kumphepo zinai za mlengalenga. Ndipo mu imodzi ya izi munaphuka nyanga yaing'ono, imene inakula kwakukulu ndithu, kuloza kumwera, ndi kum'mawa, ndi kudziko lokometsetsa. Nikula, kufikira khamu la kuthambo; ndi zina za khamulo ndi za nyenyezi inazigwetsa pansi, nizipondereza. Inde inadzikulitsa kufikira kwa kalonga wa khamulo, nimchotsera nsembe yopsereza yachikhalire, ndi pokhala malo ake opatulika panagwetsedwa. Ndipo khamulo linaperekedwa kwa iyo, pamodzi ndi nsembe yopsereza yachikhalire mwa kulakwa kwake, nigwetsa pansi choonadi, nichita chifuniro chake, nikuzika. Pamenepo ndinamva wina woyera alikunena; ndi wina woyera anati kwa iye uja wanenayo, Masomphenya a nsembe yopsereza yachikhalire, ndi cholakwa chakupululutsa cha kupereka malo opatulika ndi khamulo ziponderezedwe, adzakhala mpaka liti? Nati kwa ine, Mpaka masiku zikwi ziwiri mphambu mazana atatu usana ndi usiku; pamenepo malo opatulika adzayesedwa olungama. Ndipo kunali, nditaona masomphenyawo, ine Daniele ndinafuna kuwazindikira; ndipo taonani, panaima popenyana ndi ine ngati maonekedwe a munthu. Ndipo ndinamva mau a munthu pakati pa magombe a Ulai, naitana, nati, Gabriele, zindikiritsa munthuyu masomphenyawo. Nayandikira iye poima inepo; atadza iye tsono ndinachita mantha, ndinagwa nkhope pansi; koma anati kwa ine, Zindikira, wobadwa ndi munthu iwe, pakuti masomphenyawo anena za nthawi ya chimaliziro. Ndipo m'mene analikulankhula ndi ine ndinagwidwa ndi tulo tatikulu, nkhope yanga pansi; koma anandikhudza, nandiimiritsa pokhala inepo. Ndipo anati, Taona, ndidzakudziwitsa chimene chidzachitika pa chitsiriziro cha mkwiyowo; pakuti pa nthawi yoikika mpakutha pake. Nkhosa yamphongo waiona ya nyanga ziwiri ndizo mafumu a Mediya ndi Persiya. Ndi tonde wamanyenje ndiye mfumu ya Agriki, ndi nyanga yaikulu ili pakati pa maso ake ndiyo mfumu yoyamba. Ndi kuti zinaphuka zinai m'malo mwake mwa iyo itathyoka, adzauka maufumu anai ochokera mu mtunduwu wa anthu, koma osakhala nayo mphamvu ya uja. Ndipo potsiriza pake pa ufumu wao, atakwanira olakwa, idzauka mfumu ya nkhope yaukali yakuzindikira zinsinsi. Ndi mphamvu yake idzakhala yaikulu, koma si mphamvu yakeyake ai, nidzaononga modabwitsa, nidzakuzika, ndi kuchita, ndi kuononga amphamvuwo, ndi anthu opatulikawo. Ndipo mwa kuchenjera kwake adzapindulitsa chinyengo m'dzanja mwake, nadzadzikuza m'mtima mwake; ndipo posatekeseka anthu, adzaononga ambiri; adzaukiranso kalonga wa akalonga, koma adzathyoledwa popanda dzanja. Ndipo masomphenya a madzulo ndi mamawa adanenawo ndi oona; koma iwe ubise masomphenyawo, popeza adzachitika atapita masiku ambiri. Ndipo ine Daniele ndinakomoka ndi kudwala masiku ena; pamenepo ndinauka ndi kuchita ntchito ya mfumu; ndipo ndinadabwa nao masomphenyawo, koma panalibe wakuwazindikiritsa. Chaka choyamba cha Dariusi mwana wa Ahasuwero, wa mbeu ya Amedi, amene anamlonga mfumu ya Ababiloni; chaka choyamba cha ufumu wake, ine Daniele ndinazindikira mwa mabuku kuti chiwerengo chake cha zaka, chimene mau a Yehova anadzera nacho kwa Yeremiya mneneri, kunena za makwaniridwe a mapasuko a Yerusalemu, ndizo zaka makumi asanu ndi awiri. Ndipo ndinaika nkhope yanga kwa Ambuye Mulungu, kumfunsa Iye m'pemphero, ndi mapembedzero, ndi kusala, ndi ziguduli, ndi mapulusa. Ndipo ndinapemphera kwa Yehova Mulungu wanga ndi kuvomereza, ndi kuti, Ambuye Mulungu wamkulu ndi woopsa, wakuwasungira pangano ndi chifundo iwo akukukondani, ndi kusunga malamulo anu, tachimwa, tachita mphulupulu, tachita zoipa, tapanduka, kupatuka ndi kusiya maneno anu ndi maweruzo anu; sitinamvera atumiki anu aneneri, amene ananena m'dzina lanu kwa mafumu athu, akalonga athu, makolo athu, ndi anthu onse a m'dziko. Ambuye, chilungamo ncha Inu, koma kwa ife manyazi a nkhope yathu, monga lero lino; kwa anthu a Yuda, ndi kwa okhala m'Yerusalemu, ndi kwa Aisraele onse okhala pafupi ndi okhala kutali, kumaiko onse kumene mudawaingira, chifukwa cha kulakwa kwao anakulakwirani nako. Ambuye, kwa ife kuli manyazi a nkhope yathu, kwa mafumu athu, kwa akalonga athu, ndi kwa makolo athu; pakuti takuchimwirani. Ambuye Mulungu wathu ndiye wachifundo, ndi wokhululukira; pakuti tampandukira Iye; sitinamvera mau a Yehova Mulungu wathu, kuyenda m'malamulo ake anatiikirawo pamaso pathu, mwa atumiki ake aneneri. Inde Israele yense walakwira chilamulo chanu, ndi kupatuka, kuti asamvere mau anu; chifukwa chake temberero lathiridwa pa ife, ndi lumbiro lolembedwa m'chilamulo cha Mose mtumiki wa Mulungu; pakuti tamchimwira. Ndipo anakwaniritsa mau ake adanenawo, kutitsutsa ife ndi oweruza athu otiweruza, ndi kutitengera choipa chachikulu; pakuti pansi pa thambo lonse sipanachitika monga umo panachitikira Yerusalemu. Monga mulembedwa m'chilamulo cha Mose choipa ichi chonse chatidzera; koma sitinapepeza Yehova Mulungu wathu, ndi kubwera kuleka mphulupulu zathu, ndi kuchita mwanzeru m'choonadi chanu. Chifukwa chake Yehova wakhala maso pa choipacho, ndi kutifikitsira icho; pakuti Yehova Mulungu wathu ali wolungama mu ntchito zake zonse azichita; ndipo sitinamvera mau ake. Ndipo tsopano, Ambuye Mulungu wathu, amene munatulutsa anthu anu m'dziko la Ejipito ndi dzanja lamphamvu, ndi kudzitengera mbiri monga lero lino, tachimwa, tachita choipa. Ambuye, monga mwa chilungamo chanu chonse, mkwiyo wanu ndi ukali wanu zitembenuketu, zichoke kumudzi wanu Yerusalemu, phiri lanu lopatulika; pakuti mwa zochimwa zathu, ndi mphulupulu za makolo athu, Yerusalemu ndi anthu anu asanduka chotonza cha onse otizungulira. Ndipo tsopano, Mulungu wathu, mumvere pemphero la mtumiki wanu, ndi mapembedzero ake, nimuwalitse nkhope yanu pa malo anu opatulika amene ali opasuka, chifukwa cha Ambuye. Mulungu wanga, tcherani khutu, nimumvere, tsegulani maso anu, nimupenye zopasuka zathu, ndi mudzi udatchedwawo dzina lanu; pakuti dzina lanu; pakuti sititula mapembedzero athu pamaso panu, chifukwa cha ntchito zathu zolungama, koma chifukwa cha zifundo zanu zochuluka. Ambuye, imvani; Ambuye khululukirani; Ambuye, mverani nimuchite; musachedwa, chifukwa cha inu nokha, Mulungu wanga; pakuti mudzi wanu ndi anthu anu anatchedwa dzina lanu. Ndipo pakunena ine, ndi kupemphera, ndi kuvomereza tchimo langa, ndi tchimo la anthu a mtundu wanga Israele, ndi kutula chipembedzero changa pamaso pa Yehova Mulungu wanga, chifukwa cha phiri lopatulika la Mulungu wanga; inde pakunena ine m'kupemphera, munthu uja Gabriele, amene ndidamuona m'masomphenya poyamba paja, anauluka mwaliwiro nandikhudza ngati nthawi yakupereka nsembe ya madzulo. Ndipo anandilangiza ine, ndi kulankhula nane, nati, Daniele iwe, ndatuluka tsopano ine kukuzindikiritsa mwaluntha. Pakuyamba iwe mapembedzero ako, linatuluka lamulo; ndipo ndadza ine kukufotokozera; pakuti ukondedwa kwambiri; zindikira tsono mau awa, nulingirire masomphenyawo. Masabata makumi asanu ndi awiri alamulidwira anthu a mtundu wako ndi mudzi wako wopatulika, kumaliza cholakwacho, ndi kutsiriza machimo, ndi kutetezera mphulupulu, ndi kufikitsa chilungamo chosalekeza, ndi kukhomera chizindikiro masomphenya ndi zonenera, ndi kudzoza malo opatulika kwambiri. Dziwa tsono, nuzindikire, kuti kuyambira kutuluka lamulo lakukonzanso, ndi kummanga Yerusalemu, kufikira wodzozedwayo, ndiye kalonga, kudzakhala masabata asanu ndi awiri; ndi masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri makwalala ndi tchemba zidzamangidwanso, koma mu nthawi za mavuto. Ndipo atapita masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri wodzozedwayo adzalikhidwa, nadzakhala wopanda kanthu; ndi anthu a kalonga wakudzayo adzaononga mudzi ndi malo opatulika; ndi kutsiriza kwake kudzakhala kwa chigumula, ndi kufikira chimaliziro kudzakhala nkhondo; chipasuko chalembedweratu. Ndipo iye adzapangana chipangano cholimba ndi ambiri sabata limodzi; ndi pakati pa sabata adzaleketsa nsembe yophera ndi nsembe yaufa; ndi pa phiko la zonyansa padzafika wina wakupasula, kufikira chimaliziro cholembedweratu, mkwiyo udzatsanulidwa pa wopasulayo. Chaka chachitatu cha Kirusi mfumu ya Persiya, chinavumbulutsidwa chinthu kwa Daniele, amene anamutcha Belitesazara; ndipo chinthucho nchoona, ndicho nkhondo yaikulu; ndipo anazindikira chinthucho, nadziwa masomphenyawo. Masiku aja ine Daniele ndinali kulira masabata atatu amphumphu. Chakudya chofunika osachidya ine, nyama kapena vinyo zosapita pakamwa panga, osadzola ine konse, mpaka anakwaniridwa masabata atatu amphumphu. Ndipo tsiku la makumi awiri mphambu anai la mwezi woyamba, pokhala ine m'mphepete mwa mtsinje waukulu, ndiwo Tigrisi, ndinakweza maso anga, ndinapenya ndi kuona munthu wovala bafuta, womanga m'chuuno ndi golide woona wa ku Ufazi; thupi lake lomwe linanga berulo, ndi nkhope yake ngati maonekedwe a mphezi, ndi maso ake ngati nyali zamoto, ndi manja ake ndi mapazi ake akunga mkuwa wonyezimira, ndi kumveka kwa mau ake kunanga phokoso la aunyinji. Ndipo ine Daniele ndekha ndinaona masomphenyawo; pakuti anthu anali nane sanaone masomphenyawo; koma kunawagwera kunjenjemera kwakukulu, nathawa kubisala. Momwemo ndinatsala ndekha, ndipo ndinaona masomphenya akuluwa, koma wosakhala ndi mphamvu ine; pakuti kukoma kwanga kunasandulika chivundi mwa ine, wosakhalanso ndi chimphamvu ine. Ndipo ndinamva kunena kwa mau ake, ndipo pamene ndinamva kunena kwa mau ake ndinagwidwa ndi tulo tatikulu pankhope panga, nkhope yanga pansi. Ndipo taonani, linandikhudza dzanja ndi kundikhalitsa ndi maondo anga, ndi zikhato za manja anga. Nati kwa ine, Daniele, munthu wokondedwatu iwe, tazindikira mau ndilikunena ndi iwe, nukhale chilili; pakuti ndatumidwa kwa iwe tsopano. Ndipo pamene adanena mau awa kwa ine ndinaimirira ndi kunjenjemera. Pamenepo anati kwa ine, Usaope Daniele; pakuti kuyambira tsiku loyamba lija unaika mtima wako kuzindikira ndi kudzichepetsa pamaso pa Mulungu wako, mau ako anamveka; ndipo ndadzera mau ako. Koma kalonga wa ufumu wa Persiya ananditsekerezera njira masiku makumi awiri ndi limodzi; ndipo taonani, Mikaele, wina wa akalonga omveka, anadza kundithandiza; ndipo ndinakhala komweko ndi mafumu a Persiya. Ndadzera tsono kukuzindikiritsa chodzagwera anthu a mtundu wako masiku otsiriza; pakuti masomphenyawo ndiwo a masiku a m'tsogolo. Ndipo atanena ndi ine monga mwa mau awa, ndinaweramitsa nkhope yanga pansi ndi kukhala duu. Ndipo taonani, wina wakunga ana a anthu anakhudza milomo yanga; pamenepo ndinatsegula pakamwa panga ndi kunena naye woima popenyana nane, Mbuye wanga, chifukwa cha masomphenyawo zowawa zanga zandibwerera, ndipo ndilibenso mphamvu. Pakuti mnyamata wa mbuye wanga inu akhoza bwanji kulankhula ndi mbuye wanga inu? Pakuti ine tsopano apa mulibenso mphamvu mwa ine, osanditsaliranso mpweya. Pamenepo anandikhudzanso wina, maonekedwe ake ngati munthu, nandilimbikitsa ine. Nati, Munthu wokondedwatu iwe, Usaope, mtendere ukhale nawe; limbika, etu limbika. Ndipo pamene ananena ndi ine ndinalimbikitsidwa, ndinati, Anene mbuye wanga; pakuti mwandilimbikitsa. Pamenepo anati, Kodi udziwa chifukwa choti ndakudzera? Ndipo tsopano ndibwerera kulimbana ndi kalonga wa Persiya; ndipo pomuka ine, taonani, adzadza kalonga wa Agriki. Koma ndidzakufotokozera cholembedwa pa lemba la choonadi; ndipo palibe wina wakudzilimbikitsa pamodzi ndi ine, kutsutsana ndi aja, koma Mikaele kalonga wanu. Ndipo ine, chaka choyamba cha Dariusi Mmedi, ndinauka kumlimbikitsa ndi kumkhazikitsa. Ndipo tsopano ndikufotokozera choonadi. Taona, adzaukanso mafumu atatu m'Persiya, ndi yachinai idzakhala yolemera ndithu yoposa onsewo; ndipo itadzilimbitsa yokha mwa kulemera kwake idzawautsa onse alimbane nao ufumu wa Agriki. Ndipo idzauka mfumu yamphamvu, nidzachita ufumu ndi ulamuliro waukulu, nidzachita monga mwa chifuniro chake. Ndipo pakuuka iye ufumu wake udzathyoledwa, nudzagawikira kumphepo zinai za mlengalenga; koma sadzaulandira a mbumba yake akudza m'mbuyo, kapena monga mwa ulamuliro wake anachita ufumu nao; pakuti ufumu wake udzazulidwa, ukhale wa ena, si wa aja ai. Ndipo mfumu ya kumwera, ndiye wina wa akalonga ake, idzamposa mphamvu, nidzakhala nao ulamuliro; ulamuliro wake ndi ulamuliro waukulu. Ndipo pakutha zaka adzaphatikizana iwo; ndi mwana wamkazi wa mfumu ya kumwera adzafika kwa mfumu ya kumpoto, kupangana naye zoyenera; koma mkaziyo sadzaisunga mphamvu ya dzanja lake; ngakhale mwamunayo sadzaimika, ngakhale dzanja lake; koma mkaziyo adzaperekedwa, pamodzi ndi iwo adadza naye, ndi iye amene anambala, ndi iye amene anamlimbitsa nthawi zija. Koma apo pophukira mizu yake adzauka wina m'malo mwake, ndiye adzafika kulimbana nalo khamu la nkhondo, nadzalowa m'linga la mfumu ya kumpoto, nadzachita molimbana nao, nadzawalaka; ndi milungu yao yomwe, pamodzi ndi akalonga ao, ndi zipangizo zao zofunika zasiliva ndi golide adzazitenga kunka nazo ndende ku Ejipito; ndi zaka zake zidzaposa za mfumu ya kumpoto. Ndipo adzalowa m'ufumu wa mfumu ya kumwera, koma adzabwera m'dziko lakelake. Ndi ana ake adzachita nkhondo, nadzamemeza makamu a nkhondo akulu ochuluka, amene adzalowa, nadzasefukira, nadzapita; ndipo adzabwerera, nadzachita nkhondo mpaka linga lake. Ndi mfumu ya kumwera adzawawidwa mtima, nadzatuluka kulimbana naye, ndiye mfumu ya kumpoto imene idzaonetsa unyinji waukulu; koma unyinjiwo udzaperekedwa m'dzanja lake. Ndipo atauchotsa unyinjiwo udzakwezeka mtima wake; ndipo adzagwetsa zikwi makumimakumi, koma sadzalakika. Ndi mfumu ya kumpoto idzabwera, nidzaimika unyinji wakuposa oyamba aja; nidzafika pachimaliziro cha nthawi, cha zaka, ndi khamu lalikulu la nkhondo ndi chuma chambiri. Ndipo nthawi zija ambiri adzaukira mfumu ya kumwera, ndi achiwawa mwa anthu a mtundu wako adzadzikuza kukhazikitsa masomphenyawo, koma adzagwa iwo. Ndi mfumu ya kumpoto idzadza, nidzaunda mtumbira, nidzalanda midzi yamalinga; ndi ankhondo a kumwera sadzalimbika, ngakhale anthu ake osankhika; inde sipadzakhala mphamvu yakulimbika. Koma iye amene amdzera kulimbana naye adzachita chifuniro chake cha iye mwini; palibe wakulimbika pamaso pake; ndipo adzaima m'dziko lokometsetsalo, ndi m'dzanja mwake mudzakhala chionongeko. Ndipo adzalimbitsa nkhope yake, kudza ndi mphamvu ya ufumu wake wonse, ndi oongoka mtima pamodzi naye; ndipo adzachita chifuniro chake, nadzampatsa mwana wamkazi wa akazi kumuipitsa; koma mkaziyo sadzalimbika, kapena kuvomerezana naye. Pambuyo pake adzatembenuzira nkhope yake kuzisumbu, nadzalanda zambiri; koma kalonga wina adzaleketsa kunyoza kwake adanyoza nako; inde adzambwezera yekha kunyoza kwake. Pamenepo adzatembenuzira nkhope yake kumalinga a dziko lakelake; koma adzakhumudwa, nadzagwa osapezedwanso. Ndipo m'malo mwake adzauka wina wakupititsa wamsonkho pa ulemerero wa ufumuwo; koma atatha masiku owerengeka adzathyoledwa iye, si mwamkwiyo, kapena kunkhondo ai. Ndi m'malo mwake adzauka munthu woluluka, amene anthu sanampatse ulemu wa ufumu, koma adzafika kachetechete, nadzalanda ufumu ndi mau osyasyalika. Ndipo mwa mayendedwe ake a chigumula adzakokololedwa pamaso pake, nadzathyoledwa, ngakhale kalonga yemwe wa chipangano. Ndipo atapangana naye adzachita monyenga; pakuti adzakwera, nadzasanduka wamphamvu ndi anthu owerengeka. Adzafika kachetechete kuminda yokometsetsa ya derali, nadzachita chosachita atate ake, kapena makolo ake; adzawawazira zofunkha, ndi zankhondo, ndi chuma, nadzalingiririra malinga ziwembu zake; adzatero nthawi. Nadzautsa mphamvu yake ndi mtima wake ayambane ndi mfumu ya kumwera ndi khamu lalikulu la nkhondo; ndi mfumu ya kumwera idzachita nkhondo ndi khamu lalikulu ndi lamphamvu ndithu; koma sadzaimika, popeza adzamlingiririra ziwembu. Inde iwo akudyako chakudya chake adzamuononga; ndi ankhondo ake adzasefukira, nadzagwa ambiri ophedwa. Ndipo mafumu awa onse awiri mitima yao idzakumbuka kuchita zoipa, nadzanena bodza ali pa gome limodzi; koma osapindula nalo; pakuti kutha kwake kudzakhala pa nthawi yoikika. Ndipo adzabwerera kudziko lake ndi chuma chambiri; ndi mtima wake udzatsutsana ndi chipangano chopatulika, nadzachita chifuniro chake, ndi kubwerera kudziko lake. Pa nthawi yoikika adzabwera, nadzalowa kumwera; koma sikudzakhala monga nthawi yoyamba ija, kapena yotsirizayi. Pakuti zombo za ku Kitimu zidzafika kuyambana naye; chifukwa chake adzatenga nkhawa, nadzabwerera, nadzaipidwa mtima ndi chipangano chopatulika, nadzachita chifuniro chake; adzabweranso, nadzasamalira otaya chipangano chopatulika. Ndipo ankhondo adzamuimirira, nadzadetsa malo opatulika ndi linga lake; nadzachotsa nsembe yosalekezayo, nadzaimitsa chonyansa chopululutsacho. Ndipo akuchitira choipa chipanganocho iye adzawaipsa, ndi kuwasyasyalika; koma anthu akudziwa Mulungu wao adzalimbika mtima, nadzachita mwamphamvu. Ndipo aphunzitsi a anthu adzalangiza ambiri, koma adzagwa ndi lupanga, ndi lawi lamoto, ndi undende, ndi kufunkhidwa masiku ambiri. Ndipo pakugwa iwo adzathandizidwa ndi thandizo laling'ono; koma ambiri adzaphatikizana nao ndi mau osyasyalika. Nadzagwa aphunzitsi ena kuwayesa ndi moto, ndi kuwatsutsa, ndi kuwayeretsa, mpaka nthawi ya chitsiriziro; pakuti kukaliko kufikira nthawi yoikika. Ndipo mfumu idzachita monga mwa chifuniro chake, nidzadzikweza, ndi kudzikuza koposa milungu iliyonse nidzanena zodabwitsa pa Mulungu wa milungu, nidzapindula, mpaka udzachitidwa ukaliwo; pakuti chotsimikizika m'mtimacho chidzachitika. Ndipo sidzasamalira milungu ya makolo ake, kapena choikhumba akazi, kapena kusamalira milungu iliyonse; pakuti idzadzikuza koposa onse. Koma kumalo kwake idzachitira ulemu mulungu wa malinga; ndi mulungu amene makolo ake sanaudziwe, adzaulemekeza ndi golide, ndi siliva, ndi miyala ya mtengo wake, ndi zinthu zofunika. Ndipo adzachita molimbana ndi malinga olimba koposa, pomthandiza mulungu wachilendo; aliyense womvomereza adzamchulukitsira ulemu, nadzawachititsa ufumu pa ambiri, nadzagawa dziko mwa mtengo wake. Ndipo nthawi yotsiriza mfumu ya kumwera idzalimbana naye, ndi mfumu ya kumpoto idzamdzera ngati kamvulumvulu, ndi magaleta, ndi apakavalo, ndi zombo zambiri; nadzalowa m'maiko, nadzasefukira ndi kupitirira. Adzalowanso m'dziko lokometsetsalo ndi maiko ambiri adzapasuka; koma opulumuka dzanja lake ndi awa: Edomu, ndi Mowabu, ndi oyamba a ana a Amoni. Adzatambalitsiranso dzanja lake kumaiko; dziko la Ejipito lomwe silidzapulumuka. Ndipo adzachita mwamphamvu ndi chuma cha golide, ndi siliva, ndi zinthu zofunika zonse za Ejipito; Libiya ndi Akusi adzatsata mapazi ake. Koma mbiri yochokera kum'mawa ndi kumpoto idzamvuta; nadzatuluka iye ndi ukali waukulu kupha ndi kuononga konse ambiri. Ndipo adzamanga mahema a nyumba yachifumu yake pakati pa nyanja ndi phiri lopatulika lofunika; koma adzafikira chimaliziro chake wopanda wina wakumthandiza. Ndipo nthawi yomweyi adzauka Mikaele kalonga wamkulu wakutumikira ana a anthu a mtundu wako; ndipo padzakhala nthawi ya masautso, siinakhala yotere kuyambira mtundu wa anthu kufikira nthawi yomwe ija; ndipo nthawi yomweyo anthu ako adzapulumutsidwa, yense amene ampeza wolembedwa m'buku. Ndipo ambiri a iwo ogona m'fumbi lapansi adzauka, ena kunka kumoyo wosatha, ndi ena kumanyazi ndi mnyozo wosatha. Ndipo aphunzitsi adzawala ngati kunyezimira kwa thambo; ndi iwo otembenuza ambiri atsate chilungamo ngati nyenyezi kunthawi za nthawi. Koma iwe Daniele, tsekera mau awa, nukomere chizindikiro buku, mpaka nthawi ya chimaliziro; ambiri adzathamanga chauko ndi chauko, ndi chidziwitso chidzachuluka. Pamenepo ine Daniele ndinapenya, ndipo taonani, anaimapo awiri ena, wina m'mphepete mwa mtsinje tsidya lino, ndi mnzake m'mphepete mwa mtsinje tsidya lija. Ndipo wina anati kwa munthu wovala bafuta, wokhala pamwamba pa madzi a mumtsinje, Chimaliziro cha zodabwitsa izi chidzafika liti? Ndipo ndinamva munthuyo wovala bafuta wokhala pamwamba pa madzi a mumtsinje, nakweza dzanja lake lamanja ndi lamanzere kumwamba, nalumbira pali Iye wokhala ndi moyo kosatha, kuti zidzachitika nthawi, ndi nthawi zina, ndi nusu; ndipo atatha kumwaza mphamvu ya anthu opatulikawo zidzatha izi zonse. Ndinachimva ichi, koma osachizindikira; pamenepo ndinati Mbuye wanga, chitsiriziro cha izi nchiyani? Ndipo anati, Pita Daniele; pakuti mauwo atsekedwa, nakomeredwa chizindikiro mpaka nthawi ya chitsiriziro. Ambiri adzadzitsuka ndi kudziyeretsa, nadzayesedwa ndi moto; koma oipa adzachita moipa; ndipo palibe mmodzi wa oipa adzazindikira; koma aphunzitsi ndiwo adzazindikira. Ndipo kuyambira nthawi yoti idzachotsedwa nsembe yachikhalire, nichidzaimika chonyansa chakupululutsa, adzakhalanso masiku chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi asanu ndi anai. Wodala iye amene ayembekeza, nafikira kumasiku chikwi chimodzi mphambu mazana atatu kudza makumi atatu ndi asanu. Koma iwe, muka mpaka chimaliziro; pakuti udzapumula, nudzaima m'gawo lako masiku otsiriza. Mau a Yehova amene anadza kwa Hoseya mwana wa Beeri masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda, ndi masiku a Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele. Chiyambi cha kunena kwa Yehova mwa Hoseya. Ndipo Yehova anati kwa Hoseya, Muka, udzitengere mkazi wachigololo ndi ana achigololo; pakuti dziko latsata chigololo chokhachokha kuleka kutsata Yehova. Ndipo anamuka natenga Gomeri mwana wamkazi wa Dibulaimu; iye naima, nambalira mwana wamwamuna. Ndipo Yehova anati kwa iye, Umutche dzina lake Yezireele; pakuti katsala kanthawi, ndipo ndidzabwezera chilango mwazi wa Yezireele pa nyumba ya Yehu, ndi kuleketsa ufumu wa nyumba ya Israele. Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ndidzathyola uta wa Israele m'chigwa cha Yezireele. Ndipo anaimanso, nabala mwana wamkazi. Ndipo Yehova anati kwa iye, Umutche dzina lake Wosachitidwa-chifundo; pakuti sindidzachitiranso chifundo nyumba ya Israele, kuti ndiwakhululukire konse. Koma ndidzachitira chifundo nyumba ya Yuda, ndi kuwapulumutsa mwa Ine Yehova Mulungu wao, osawapulumutsa ndi uta, kapena lupanga, kapena nkhondo ndi akavalo, kapena apakavalo. Ataleka tsono kuyamwitsa Wosachitidwa-chifundo, anaima, nabala mwana wamwamuna. Ndipo Yehova anati, Umutche dzina lake Si-anthu-anga; pakuti inu sindinu anthu anga, ndipo Ine sindine wanu. Angakhale anatero, kuwerenga kwake kwa ana a Israele kudzanga mchenga wa kunyanja, wosayeseka kapena kuwerengeka; ndipo kudzatero kuti m'mene adawanena, Simuli anthu anga, adzanena nao, Muli ana a Mulungu wamoyo. Ndipo ana a Yuda ndi ana a Israele adzasonkhanidwa pamodzi, nadzadziikira mkulu mmodzi, nadzakwera kuchoka m'dziko; pakuti tsiku la Yezireele ndi lalikulu. Nenani kwa abale anu, Anthu anga, ndi kwa alongo anu, Wochitidwa-chifundo. Mutsutsane naye mai wanu, mutsutsane naye; pakuti sali mkazi wanga, ndi Ine sindili mwamuna wake; ndipo achotse zadama zake pankhope pake, ndi zigololo zake pakati pa mawere ake; ndingamvule wamaliseche, ndi kumuika ngati tsiku lija anabadwalo, ndi kumsanduliza ngati chipululu, ndi kumuika ngati dziko louma, ndi kumupha nalo ludzu; ndipo ana ake sindidzawachitira chifundo; pakuti iwo ndiwo ana achigololo. Pakuti mai wao anachita chigololo; iye amene anali ndi pakati pa iwo anachita chamanyazi; pakuti anati, Ndidzatsata ondikondawo, akundipatsa ine chakudya changa, ndi madzi anga, ubweya wanga, ndi thonje langa, mafuta anga, ndi chakumwa changa. Chifukwa chake taonani, ndidzatchinga njira yako ndi minga, ndipo ndidzammangira mpanda, kuti asapeze mabande ake. Ndipo adzatsata omkonda koma osawagwira, adzawafunafuna koma osawapeza; pamenepo adzati, Ndidzamuka ndi kubwererana ndi mwamuna wanga woyamba, popeza pamenepo panandikomera koposa tsopano. Pakuti sanadziwa kuti ndine ndinampatsa tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi kumchulukitsira siliva ndi golide, zimene anapanga nazo Baala. Chifukwa chake ndidzabwera ndi kuchotsa tirigu wanga m'nyengo yake, ndi vinyo wanga m'nthawi yake yoikika, ndi kukwatula ubweya wanga ndi thonje langa, zimene zikadafunda umaliseche wake. Ndipo tsopano ndidzaonetsa manyazi ake pamaso pa omkonda, popandanso wakumlanditsa m'dzanja langa. Ndidzaleketsanso kusekerera kwake konse, zikondwerero zake, pokhala mwezi pake, ndi masabata ake, ndi masonkhano ake onse oikika. Ndipo ndidzapasula mipesa yake ndi mikuyu yake, imene adanena, Iyi ndi mphotho yanga anandipatsa ondikondawo; ndipo ndidzaisandutsa thengo, ndi nyama za kuthengo zidzaidya. Ndipo ndidzamlanga chifukwa cha masiku a Abaala amene anawafukizira, navala mphete za m'mphuno, ndi zokometsera zake, natsata omkonda, nandiiwala Ine, ati Yehova. Chifukwa chake taonani, ndidzamkopa ndi kunka naye kuchipululu, ndi kulankhula naye momkonda mtima. Ndipo ndidzampatsa minda yake yamphesa kuyambira pomwepo, ndi chigwa cha Akori chikhale khomo la chiyembekezo; ndipo adzavomereza pomwepo monga masiku a ubwana wake, ndi monga tsiku lokwera iye kutuluka m'dziko la Ejipito. Ndipo kudzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova, udzanditcha Mwamuna wanga, osanditchanso Baala wanga. Pakuti ndidzachotsa maina a Abaala m'kamwa mwake; ndipo silidzakumbukikanso dzina lao. Ndipo tsiku lomwelo ndidzawachitira pangano ndi nyama za kuthengo, ndi mbalame za mlengalenga, ndi zokwawa pansi; ndipo ndidzathyola uta, ndi lupanga, ndi nkhondo, zichoke m'dziko, ndi kuwagonetsa pansi mosatekeseka. Ndipo ndidzakutomera ukhale wanga kosatha, inde ndidzakutomera ukhale wanga m'chilungamo, ndi m'chiweruzo, ndi m'ukoma mtima, ndi m'chifundo. Ndidzakutomeranso ukhale wanga mokhulupirika, ndipo udzadziwa Yehova. Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ndidzavomereza, ati Yehova, ndidzavomereza thambo, ndi ilo lidzavomereza dziko lapansi; ndi dziko lapansi lidzavomereza tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; ndi izi zidzavomereza Yezireele. Ndipo ndidzadzibzalira iye m'nthaka, ndipo ndidzachitira chifundo Wosachitidwa-chifundo; ndipo ndidzati kwa Si-anthu-anga, Muli anthu anga; ndipo iwo adzati, Ndinu Mulungu wathu. Ndipo Yehova anati kwa ine, Mukanso, konda mkazi wokondedwa ndi bwenzi lake, koma wakuchita chigololo, monga Yehova akonda ana a Israele, angakhale atembenukira kumilungu ina, nakonda nchinchi za mphesa zouma. M'mwemo ndinadzigulira iye ndi masekeli khumi ndi asanu a siliva, ndi homeri ndi leteki wa barele; ndipo ndinati kwa iye, Uzikhala ndi ine masiku ambiri, usachita chigololo, usakhala mkazi wa mwamuna aliyense; momwemo inenso nawe. Pakuti ana a Israele adzakhala masiku ambiri opanda mfumu, ndi opanda kalonga, ndi opanda nsembe, ndi opanda choimiritsa, ndi opanda efodi kapena aterafi; atatero ana a Israele adzabwera, nadzafuna Yehova Mulungu wao, ndi Davide mfumu yao, nadzafika ndi mantha kwa Yehova, ndi ku ukoma wake masiku otsiriza. Imvani mau a Yehova, inu ana a Israele; pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi okhala m'dziko, popeza palibe choonadi, kapena chifundo, kapena kudziwa Mulungu m'dziko. Koma kulumbira, ndi kunama, ndi kupha, ndi kuba, ndi kuchita chigololo; aboola, ndi mwazi ukhudzana nao mwazi. Chifukwa chake dziko lidzachita chisoni, ndi aliyense wokhalamo adzalefuka, pamodzi ndi nyama za kuthengo, ndi mbalame za m'mlengalenga; ndi nsomba za m'nyanja zomwe zidzachotsedwa. Koma munthu asatsutsane ndi mnzake, kapena kudzudzula mnzake; popeza anthu ako ndiwo akunga otsutsana ndi wansembe. Ndipo udzakhumudwa usana, ndi mneneri yemwe adzakhumudwa pamodzi ndi iwe usiku; ndipo ndidzaononga mai wako. Anthu anga aonongeka chifukwa cha kusadziwa; popeza unakana kudziwa, Inenso ndikukaniza, kuti usakhale wansembe wanga; popeza waiwala chilamulo cha Mulungu wako, Inenso ndidzaiwala ana ako. Monga anachuluka, momwemo anandichimwira; ndidzasanduliza ulemerero wao ukhale manyazi. Adyerera tchimo la anthu anga, nakhumbira chosalungama chao, yense ndi mtima wake. Ndipo kudzakhala monga anthu, momwemo wansembe; ndipo ndidzawalanga chifukwa chanjira zao, ndi kuwabwezera machitidwe ao. Ndipo adzadya, koma osakhuta; adzachita chigololo, koma osachuluka; pakuti waleka kusamalira Yehova. Chigololo, ndi vinyo, ndi vinyo watsopano, zichotsa mtima. Anthu anga afunsira kumtengo wao, ndi ndodo yao iwafotokozera; pakuti mzimu wachigololo wawalakwitsa, ndipo achita chigololo kuchokera Mulungu wao. Pamwamba pa mapiri aphera nsembe, nafukiza pazitunda, patsinde pa thundu, ndi minjali, ndi mkundi; popeza mthunzi wake ndi wabwino, chifukwa chake ana anu akazi achita uhule, ndi apongozi anu achita chigololo. Sindidzalanga ana anu akazi pochita iwo uhule, kapena apongozi anu pochita chigololo iwo; pakuti iwo okha apatukira padera ndi akazi achiwerewere, naphera nsembe pamodzi ndi akazi operekedwa ku uhule; ndi anthu osazindikirawo adzagwetsedwa chamutu. Chinkana iwe, Israele, uchita uhule, koma asapalamule Yuda; ndipo musafika inu ku Giligala, kapena kukwera ku Betaveni, kapena kulumbira, Pali Yehova. Pakuti Israele wachita kuuma khosi ngati ng'ombe yaikazi yaing'ono youma khosi; tsopano Yehova adzawadyetsa ngati mwanawankhosa kuthengo lalikulu. Efuremu waphatikana ndi mafano, mlekeni. Chakumwa chao chasasa, achita uhule kosalekeza; akulu ao akonda manyazi kwambiri. Mphepo yamkulunga m'mapiko ake, ndipo adzachita manyazi chifukwa cha nsembe zao. Imvani ichi, ansembe inu; mverani, inu nyumba ya Israele; tcherani khutu, inu nyumba ya mfumu; pakuti chiweruzochi chinena inu; pakuti munakhala msampha ku Mizipa, ndi ukonde woyalidwa pa Tabori. Ndipo opandukawo analowadi m'zovunda; koma Ine ndine wakuwadzudzula onsewo. Ndimdzaiwa Efuremu, ndi Israele sandibisikira; pakuti Efuremu iwe, wachita uhule tsopano, Israele wadetsedwa. Machitidwe ao sawalola kubwerera kwa Mulungu wao; pakuti mzimu wa uhule uli m'kati mwao, ndipo sadziwa Yehova. Ndipo kudzikuza kwa Israele kudzamchitira umboni pamaso pake; chifukwa chake Israele ndi Efuremu adzakhumudwa m'mphulupulu mwao; Yudanso adzakhumudwa pamodzi nao. Adzamuka ndi zoweta zao zazing'ono ndi zazikulu kufunafuna Yehova: koma sadzampeza; Iye wadzibweza kuwachokera. Anachita mosakhulupirika pa Yehova, pakuti anabala ana achilendo; mwezi wokhala udzawatha tsopano, pamodzi ndi maiko ao. Ombani mphalasa m'Gibea, ndi lipenga m'Rama; fuulani ku Betaveni; pambuyo pako, Benjamini. Efuremu adzasanduka bwinja tsiku lakudzudzula; mwa mafuko a Israele ndadziwitsa chodzachitikadi. Akalonga a Yuda akunga anthu osuntha malire; ndidzawatsanulira mkwiyo wanga ngati madzi. Efuremu azunzika, apsinjika pa mlanduwo; pakuti anafuna mwini wake kutsata lamulolo. Ndipo ndikhala kwa Efuremu ngati njenjete, ndi kwa nyumba ya Yuda ngati chivundi. Pamene Efuremu anaona nthenda yake, ndi Yuda bala lake, Efuremu anamuka kwa Asiriya, natumiza kwa mfumu Yarebu; koma iye sakhoza kukuchiritsani, kapena kupoletsa bala lanu. Pakuti ndidzakhala kwa Efuremu ngati mkango, ndi kwa nyumba ya Yuda ngati msona wa mkango; ndidzamwetula Ine ndi kuchoka; ndidzanyamula, ndipo palibe wakulanditsa. Ndidzamuka ndi kubwerera kunka kumalo kwanga, mpaka adzavomereza kupalamula kwao, nafunafuna nkhope yanga; m'msauko mwao adzandifunafuna mwachangu. Tiyeni, tibwerere kunka kwa Yehova; pakuti wang'amba, nadzatipoletsera; wakantha, nadzatimanga. Atapita masiku awiri adzatitsitsimutsa, tsiku lachitatu adzatiutsa; ndipo tidzakhala ndi moyo pamaso pake. Tidziwe tsono, tilondole kudziwa Yehova; kutuluka kwake kwakonzekeratu ngati matanda kucha; ndipo adzatidzera ngati mvula, ngati mvula ya masika yakuthirira dziko. Efuremu iwe, ndidzakuchitira chiyani? Yuda iwe, ndikuchitire chiyani? Pakuti kukoma mtima kwako kukunga mtambo wam'mawa ndi ngati mame akuphawa mamawa. Chifukwa chake ndawalikha mwa aneneri; ndawapha ndi mau a pakamwa panga; ndi maweruzo anga atuluka ngati kuunika. Pakuti ndikondwera nacho chifundo, si nsembe ai; ndi kumdziwa Mulungu kuposa nsembe zopsereza. Koma iwo analakwira chipangano ngati Adamu, m'mene anandichitira monyenga. Giliyadi ndiwo mudzi wa ochita zoipa, wa mapazi a mwazi. Ndipo monga magulu a mbala alalira munthu, momwemo msonkhano wa ansembe amapha pa njira ya ku Sekemu; indedi achita choipitsitsa. M'nyumba ya Israele ndinaona chinthu choopsetsa; pamenepo pali uhule wa Efuremu; Israele wadetsedwa. Akuikidwiratunso nyengo yakukolola, Yuda iwe, pamene ndikabwezanso undende wa anthu anga. M'mene ndichiritsa Israele, mphulupulu ya Efuremu ivumbuluka, ndi zoipa za Samariya; pakuti achita bodza, ndipo mkhungu alowa m'nyumba, ndi gulu la mbala lilanda kubwalo. Ndipo sanena m'mtima mwao kuti Ine ndikumbukira zoipa zao zonse; tsopano machitidwe ao awazinga; ali pamaso panga. Akondweretsa mfumu ndi zoipa zao, ndi akalonga ndi mabodza ao. Achigololo onsewo; akunga ng'anjo anaitenthetsa woocha mkate; aleka kusonkha moto, poyambira kukanda mtanda kufikira watupa mtandawo. Tsiku la mfumu yathu akalonga adzidwalitsa ndi kutentha kwa vinyo; iye anatambasula dzanja lake pamodzi ndi oseka. Pakuti asendera nao mtima wao wakunga ng'anjo ya mkate, pokhala alikulalira; woocha mkate wao agona usiku wonse, m'mawa iyaka ngati moto wa malawi. Onsewo atentha ngati ng'anjo, natha oweruza ao, agwa mafumu ao onse; palibe mmodzi mwa iwo wakuitana Ine. Efuremu asokonezana nayo mitundu ya anthu; Efuremu ndiye kamtanda ka mkate kosatembenuzidwa. Alendo anatha mphamvu yake osachidziwa iye; imvi zomwe zampakiza osachidziwa iye. Ndipo kudzikuza kwa Israele kumchitira umboni pamaso pake; koma sanabwerere kunka kwa Yehova Mulungu wao, kapena kumfunafuna mwa ichi chonse. Ndipo Efuremu ali ngati nkhunda yopusa yopanda nzeru; aitanira kwa Ejipito, amuka kwa Asiriya. Pamene amuka ndidzawayalira ukonde wanga, ndidzawagwetsa ngati mbalame za m'mlengalenga, ndidzawalanga monga udamva msonkhano wao. Tsoka kwa iwowa! Pakuti anandizembera; chionongeko kwa iwowa! Pakuti anandilakwira; ndikadawalanditsa Ine, koma anandinenera zabodza. Ndipo sanafuulire kwa Ine ndi mtima wao, koma alira pakama pao, asonkhanira tirigu ndi vinyo, apikisana ndi Ine. Chinkana ndawalangiza ndi lulimbitsa manja ao, andilingiririra choipa. Abwerera, koma si kwa Wam'mwambayo; akunga uta wosakhulupirika; akalonga ao adzagwa ndi lupanga mwa chipongwe cha lilime lao; ichi ndicho adzawasekera m'dziko la Ejipito. Lipenga kukamwa kwako. Akudza ngati chiombankhanga, kulimbana ndi nyumba ya Yehova; chifukwa analakwira chipangano changa, napikisana nacho chilamulo changa. Adzafuulira kwa Ine, Mulungu wanga, ife Aisraele tikudziwani. Israele wachitaya chokoma, mdani adzamlondola. Analonga mafumu, koma sikunachokera kwa Ine; anaika akalonga, koma sindinadziwa; anadzipangira mafano a siliva wao ndi golide wao, kuti akalikhidwe. Mwanawang'ombe wako wakutaya, Samariya iwe; mkwiyo wanga wayakira iwo; adzalephera kuyera mtima mpaka liti? Pakuti ichi chomwe chafumira kwa Israele; mmisiri wampanga, koma sali Mulungu; inde mwanawang'ombe wa Samariya adzaphwanyikaphwanyika. Pakuti abzala mphepo, nadzakolola kamvulumvulu; alibe tirigu wosasenga; ngala siidzatulutsa ufa; chinkana iutulutsa, alendo adzaumeza. Israele wamezedwa; tsopano ali mwa amitundu ngati chotengera choti munthu sakondwera nacho. Pakuti anakwera kunka ku Asiriya, ngati mbidzi ya pa yokha mwini wake; Efuremu walembera omkonda ngati antchito. Inde angakhale alembera mwa amitundu ndidzawasonkhanitsa tsopano; ndipo ayamba kuchepa chifukwa cha katundu wa mfumu ya akalonga. Popeza Efuremu anachulukitsa maguwa a nsembe akuchimwako, maguwa a nsembe omwewo anamchimwitsa. Ndinamlembera zinthu zambirimbirizo za chilamulo changa, koma zinayesedwa ngati chinthu chachilendo. Kunena za nsembe za zopereka zanga, aphera nsembe yanyama, naidya; koma Yehova sazilandira; tsopano adzakumbukira mphulupulu yao, nadzalanga zochimwa zao; adzabwerera kunka ku Ejipito. Pakuti Israele waiwala Mlengi wake, namanga akachisi; ndipo Yuda wachulukitsa midzi yamalinga; koma ndidzatumizira midzi yake moto, nudzatha nyumba zake zazikulu. Usakondwera, Israele, ndi kusekerera, ngati mitundu ya anthu; pakuti wachita chigololo kuleka Mulungu wako, wakonda mphotho ya chigololo pa dwale la tirigu lililonse. Dwale ndi choponderamo mphesa sizidzawadyetsa, vinyo watsopano adzamsowa. Sadzakhala m'dziko la Yehova; koma Efuremu adzabwerera kunka ku Ejipito; ndipo adzadya chakudya chodetsa m'Asiriya. Sadzatsanulira Yehova nsembe zavinyo; sizidzamkomera Iye nsembe zao; zidzakhala kwa iwo ngati mkate wa achisoni; onse akudyako adzadetsedwa; pakuti mkate wao udzakhala wa njala yao, uwu sudzalowa m'nyumba ya Yehova. Mudzachitanji tsiku la masonkhano oikika, ndi tsiku la chikondwerero cha Yehova. Pakuti taonani, anachokera chionongeko, koma Ejipito adzawasonkhanitsa, Mofi adzawaika m'manda; khwisa adzalanda zofunika zao zasiliva; minga idzakhala m'mahema mwao. Masiku a kulanga afika, masiku a kubwezera afika; Israele adzadziwa; mneneri ali wopusa, munthu wamzimu ali wamisala, chifukwa cha kuchuluka mphulupulu yako, ndi popeza udani ndi waukulu. Efuremu ndiye wozonda kwa Mulungu wanga; kunena za mneneri, msampha wa msodzi uli m'njira zake zonse, ndi udani m'nyumba ya Mulungu wake. Anadzivunditsa kwambiri, monga masiku a Gibea; adzakumbukira mphulupulu yao, adzalanga zochimwa zao. Ndinapeza Israele ngati mphesa m'chipululu, ndinaona makolo anu ngati chipatso choyamba cha mkuyu nyengo yake yoyamba; koma anadza kwa Baala-Peori, nadzipatulira chonyansacho, nasandulika onyansa, chonga chija anachikonda. Kunena za Efuremu, ulemerero wao udzauluka ndi kuchoka ngati mbalame; sipadzakhala kubala, ndi kukhala ndi pakati, ndi kuima. Angakhale alera ana ao, koma ndidzawasowetsa, wosatsala munthu; ndithunso tsoka iwowa, pamene ndiwachokera. Efuremu, monga ndaona, akunga Tiro, wookedwa pokoma; koma Efuremu adzatulutsira ana ake wakuwaphera. Apatseni, Yehova; mudzapatsa chiyani? Muwapatse mimba yotayataya, ndi mawere ouma. Choipa chao chonse chili m'Giligala; pakuti pamenepo ndinawada, chifukwa cha kuipa kwa machitidwe ao ndidzawainga kuwachotsa m'nyumba mwanga; sindidzawakondanso; akalonga ao onse ndiwo opanduka. Efuremu wakanthidwa, muzu wao wauma, iwo sadzabala zipatso; inde ngakhale abala, koma ndidzapha zipatso zofunika za mimba yao. Mulungu wanga adzawataya, pakuti sanammvere Iye; ndipo adzakhala othawathawa mwa amitundu. Israele ndi mpesa wotambalala, wodzibalira wokha zipatso; monga umo zinachulukira zipatso zake, momwemo anachulukitsa maguwa a nsembe ake; monga mwa kukoma kwake kwa dziko lake anapanga zoimiritsa zokoma. Mtima wao wagawikana, tsopano adzapezeka opalamula, adzapasula maguwa ao a nsembe, nadzaononga zoimiritsa zao. Pakuti tsopano adzati, Tilibe mfumu, popeza sitiopa Yehova; ndi mfumu idzatichitira chiyani? Anena mau akulumbira monama, pakuchita mapangano momwemo; chiweruzo chiphuka ngati zitsamba zowawa m'michera ya munda. Okhala m'Samariya adzaopera chifanizo cha anaang'ombe a ku Betaveni; pakuti anthu ake adzamva nacho chisoni, ndi ansembe ake amene anakondwera nacho, chifukwa cha ulemerero wake, popeza unachichokera. Adzachitengeranso ku Asiriya chikhale mphatso ya kwa mfumu Yarebu; Efuremu adzatenga manyazi, ndi Israele adzachita manyazi ndi uphungu wake. Ndipo Samariya, mfumu yake yamwelera ngati thovu pamadzi. Ndipo misanje ya Aveni, ndiyo tchimo la Israele, idzaonongeka; minga ndi mitungwi idzamera pa maguwa ao a nsembe; ndipo adzati kwa mapiri, Tiphimbeni; ndi kwa zitunda, Tigwereni. Israele, wachimwa kuyambira masiku a Gibea; pomwepo anaimabe; nkhondo ya ana a chosalungama siinawapeza ku Gibea. Pamene ndifuna ndidzawalanga, ndi mitundu ya anthu idzawasonkhanira pomangidwa iwo pa zolakwa zao ziwiri. Ndipo Efuremu ndiye ng'ombe yaikazi yaing'ono, yozereweredwa, yokonda kupuntha tirigu; koma ndapita pa khosi lake lokoma; ndidzamsenzetsa Efuremu goli; Yuda adzalima, Yakobo adzaphwanya chibuluma chake. Mudzibzalire m'chilungamo mukolole monga mwa chifundo; limani masala anu, pakuti yafika nthawi ya kufuna Yehova, mpaka afika Iye, navumbitsira inu chilungamo. Mwalima choipa, mwakolola chosalungama, mwadya zipatso za mabodza; pakuti watama njira yako ndi kuchuluka kwa anthu ako amphamvu. Momwemo phokoso lidzaukira anthu ako, ndi malinga ako onse adzapasuka, monga Salimani anapasula Betaribele; tsiku la nkhondo amai anaphwanyika pamodzi ndi ana ake. Momwemo adzakuchitirani Betele, chifukwa cha choipa chanu chachikulu; mbandakucha mfumu ya Israele idzalikhika konse. Pamene Israele anali mwana, ndinamkonda, ndinaitana mwana wanga ali m'Ejipito. Monga anawaitana, momwemo anawachokera; anaphera nsembe Abaala, nafukizira mafano osema. Koma Ine ndinaphunzitsa Efuremu kuyenda, ndinawafungata m'manja mwanga; koma sanadziwe kuti ndinawachiritsa. Ndinawakoka ndi zingwe za munthu, ndi zomangira za chikondi; ndinakhala nao ngati iwo akukweza goli pampuno pao, ndipo ndinawaikira chakudya. Iye sadzabwerera kunka kudziko la Ejipito, koma Asiriya adzakhala mfumu yake, popeza anakana kubwera. Ndi lupanga lidzagwera midzi yake, lidzatha mipiringidzo yake, ndi kuononga chifukwa cha uphungu wao. Ndipo anthu anga alimbika kubwerera m'mbuyo kundileka Ine; chinkana akawaitana atsate Iye ali m'mwamba, sadzakweza ndi mmodzi yense. Ndidzakusiya bwanji, Efuremu? Ndidzakupereka bwanji, Israele? Ndidzakuyesa bwanji ngati Adima? Ndidzakuika bwanji ngati Zeboimu? Mtima wanga watembenuka m'kati mwanga, zachifundo zanga zilira zonse pamodzi. Sindidzachita mkwiyo wanga waukali, sindidzabwerera kuononga Efuremu; pakuti Ine ndine Mulungu, si munthu ai; Woyera wa pakati pako; ndipo sindidzalowa m'mudzi. Adzatsata Yehova, Iye adzabangula ngati mkango; pamene abangula, ana adzafika ndi kunjenjemera kuchokera kumadzulo. Adzafika ndi kunjenjemera ngati mbalame ya ku Ejipito, ndi ngati nkhunda m'dziko la Asiriya; ndipo ndidzawakhalitsa m'nyumba zao, ati Yehova Efuremu andizinga ndi bodza, ndi nyumba ya Israele ndi chinyengo, ndi Yuda apikisana ndi Mulungu, ndiye Woyera wokhulupirika. Efuremu akudya mphepo, natsata mphepo ya kum'mawa; tsiku lonse achulukitsa mabodza ndi chipasuko, ndipo achita pangano ndi Asiriya, natenga mafuta kunka nao ku Ejipito. Ndipo Yehova ali ndi mlandu ndi Yuda, nadzalanga Yakobo monga mwa njira zake, adzambwezera monga mwa machitidwe ake. M'mimba anagwira kuchitende cha mkulu wake, ndipo atakula mphamvu analimbana ndi Mulungu; inde, analimbana ndi wamthenga nampambana; analira, nampembedza Iye; anampeza Iye ku Betele, ndi kumeneko Iye analankhula ndi ife; ndiye Yehova Mulungu wa makamu, chikumbukiro chake ndi Yehova. M'mwemo utembenukire kwa Mulungu wako, sunga chifundo ndi chiweruzo, nuyembekezere Mulungu wako kosalekeza. Ndiye Mkanani, m'dzanja lake muli miyeso yonyenga, akonda kusautsa. Ndipo Efuremu anati, Zedi ndasanduka wolemera, ndadzionera chuma m'ntchito zonse ndinazigwira; sadzapeza mwa ine mphulupulu yokhala tchimo. Koma Ine ndine Yehova Mulungu wako chichokere dziko la Ejipito, ndidzakukhalitsanso m'mahema, monga masiku a zikondwerero zoikika. Ndalankhulanso ndi aneneri, ndipo Ine ndachulukitsa masomphenya; ndi pa dzanja la aneneri ndinanena ndi mafanizo. Kodi Giliyadi ndiye wopanda pake? Akhala achabe konse; m'Giligala aphera nsembe ya ng'ombe; inde maguwa ao a nsembe akunga miulu yamiyala m'michera ya munda. Ndipo Yakobo anathawira kuthengo la Aramu, ndi Israele anagwira ntchito chifukwa cha mkazi, ndi chifukwa cha mkazi anaweta nkhosa. Ndipo mwa mneneri Yehova anakweretsa Israele kuchokera m'Ejipito, ndi mwa mneneri anasungika. Efuremu wautsa mkwiyo wowawa, m'mwemo Iye adzamsiyira mwazi wake, ndi Ambuye wake adzambwezera chomtonza chake. Pamene Efuremu analankhula panali kunjenjemera; anadzikweza m'Israele; koma pamene anapalamula mwa Baala, anafa. Ndipo tsopano aonjeza kuchimwa, nadzipangira mafano oyenga a siliva wao, mafano monga mwa nzeru zao, onsewo ntchito ya amisiri; anena za iwo, Anthu ophera nsembe apsompsone anaang'ombe. Chifukwa chake adzakhala ngati mtambo wa m'mawa, ndi ngati mame asansuka mamawa, ngati mungu umene mphepo iuuluza kudwale, ndi ngati utsi wotuluka kukafwambira. Koma Ine ndiye Yehova Mulungu wako chichokere m'dziko la Ejipito, ndipo suyenera kudziwa mulungu wina koma Ine; ndi popanda Ine palibe mpulumutsi. Ndinakudziwa m'chipululu, m'dziko lotentha kwambiri. Monga mwa podyetsa pao, momwemo anakhuta; anakhuta, ndi mtima wao unakwezeka; chifukwa chake anandiiwala Ine. Chifukwa chake ndikhala nao ngati mkango; ngati nyalugwe ndidzalalira kunjira. Ndidzakomana nao ngati chimbalangondo chochilanda ana ake, ndi kung'amba chokuta mtima wao; ndi pomwepo ndidzawalusira ngati mkango; chilombo chidzawamwetula. Israele, chikuononga ndi ichi, chakuti utsutsana ndi Ine, chithandizo chako. Ili kuti mfumu yako tsopano, kuti ikupulumutse m'midzi yako yonse? Ndi oweruza ako amene unanena za iwo, Ndipatseni mfumu ndi akalonga? Ndinakupatsa mfumu mu mkwiyo wanga; ndinamchotsanso m'ukali wanga. Mphulupulu ya Efuremu yamangika, tchimo lake lisungika. Zowawa zonga za mkazi wobala zidzamgwera, ndiye mwana wopanda nzeru; pakuti pali nyengo yakuti asachedwe mobalira ana. Ndidzawaombola kumphamvu ya kumanda, ndidzawaombola kuimfa; imfa, miliri yako ili kuti? Kulekerera kudzabisika pamaso panga. Chinkana abala mwa abale ake, mphepo ya kum'mawa idzafika, mphepo ya Yehova yokwera kuchokera kuchipululu; ndi gwero lake lidzaphwa, ndi kasupe wake adzauma, adzafunkha chuma cha akatundu onse ofunika. Samariya adzasanduka wabwinja, pakuti anapandukana ndi Mulungu wake; iwo adzagwa ndi lupanga, ana ao amakanda adzaphwanyika, ndi akazi ao okhala ndi pakati adzatumbulidwa. Israele, bwerera kunka kwa Yehova Mulungu wako; pakuti wagwa mwa mphulupulu yako. Mukani nao mau, nimubwerere kwa Yehova; nenani kwa Iye, Chotsani mphulupulu zonse, nimulandire chokoma; ndipo tidzapereka mau milomo yathu ngati ng'ombe. Asiriya sadzatipulumutsa; sitidzayenda pa akavalo, ndipo sitidzanenanso kwa ntchito ya manja athu, Inu ndinu milungu yathu; pakuti mwa Inu ana amasiye apeza chifundo. Ndidzachiritsa kubwerera kwao, ndidzawakonda mwaufulu; pakuti mkwiyo wanga wamchokera. Ndidzakhala kwa Israele ngati mame; adzachita maluwa ngati kakombo, ndi kutambalalitsa mizu yake ngati Lebanoni. Nthambi zake zidzatambalala, ndi kukoma kwake kudzanga kwa mtengo wa azitona, ndi fungo lake ngati Lebanoni. Iwo okhala pansi pa mthunzi wake adzabwera, nadzatsitsimuka ngati tirigu, nadzaphuka ngati mpesa, chikumbukiro chake chidzanga vinyo wa Lebanoni. Efuremu adzati, Ndili ndi chiyaninso ndi mafano? Ndayankha, ndidzampenyerera; ndili ngati mtengo wamlombwa wabiriwiri; zipatso zako zipezeka zochokera kwa Ine. Wanzeru ndani, kuti azindikire izi? Waluntha, kuti adziwe izi? Pakuti njira za Yehova zili zoongoka; ndipo olungama adzayendamo, koma olakwa adzagwamo. Mau a Yehova a kwa Yowele mwana wa Petuwele. Imvani ichi, akuluakulu inu, nimutchere khutu, inu nonse okhala m'dziko. Chachitika ichi masiku anu kodi, kapena masiku a makolo anu? Mufotokozere ana anu ichi, ndi ana anu afotokozere ana ao, ndi ana ao afotokozere mbadwo wina. Chosiya chimbalanga, dzombe lidachidya; ndi chosiya dzombe, chirimamine adachidya; ndi chosiya chirimamine, anoni adachidya. Galamukani, oledzera inu, nimulire; bumani, nonse akumwa vinyo, chifukwa cha vinyo watsopano; pakuti waletsedwa pakamwa panu. Pakuti mtundu wadza, wakwerera dziko langa, wamphamvu wosawerengeka, mano ake akunga mano a mkango, nukhala nao mano achibwano a mkango waukulu. Unaonongadi mpesa wanga, nunyenya mkuyu wanga, nukungudza konse, nuutaya; nthambi zake zasanduka zotumbuluka. Lirani ngati namwali wodzimangira m'chuuno chiguduli, chifukwa cha mwamuna wa unamwali wake. Nsembe yaufa ndi nsembe yothira zalekeka kunyumba ya Yehova; ansembe, atumiki a Yehova, achita maliro. M'munda mwaonongeka, nthaka ilira; pakuti tirigu waonongeka, vinyo watsopano wamwelera, mafuta akudza pang'onong'ono. Gomani, akulima m'minda inu; lirani, akulima mpesa; chifukwa cha tirigu ndi barele; pakuti dzinthu za m'minda zatayika. Mpesa wauma, mkuyu wafota, mtengo wa mkangaza ndi kanjedza ndi muula, inde mitengo yonse ya kuthengo yafota; pakuti chimwemwe chathera ana a anthu. Mudzimangire chiguduli m'chuuno mwanu, nimulire, ansembe inu; bumani otumikira kuguwa la nsembe inu; lowani, gonani usiku wonse m'chiguduli, inu otumikira Mulungu wanga; pakuti nsembe yaufa ndi nsembe yothira zaletsedwera nyumba ya Mulungu wanu. Patulani tsiku losala, lalikirani masonkhano oletsa, sonkhanitsani akuluakulu, ndi onse okhala m'dziko, kunyumba ya Yehova Mulungu wanu; nimufuulire kwa Yehova. Kalanga ine, tsikuli! Pakuti layandikira tsiku la Yehova, lidzafika ngati chionongeko chochokera kwa Wamphamvuyonse. Chakudya sichichotsedwa kodi pamaso pathu? Chimwemwe ndi chikondwerero pa nyumba ya Mulungu wathu? Mbeu zaola pansi pa zibuluma zao; zosungiramo zaonongeka, nkhokwe zapasuka; pakuti tirigu wakwinyata. Ha! Nyama ziusa moyo, magulu a ng'ombe azimidwa; pakuti zisowa podyera; magulu a nkhosa omwe atha. Ndifuulira kwa Inu Yehova, pakuti moto wapsereza mabusa a m'chipululu, ndi malawi a moto anatentha mitengo yonse ya kuthengo. Inde nyama zakuthengo zilira kwa Inu; pakuti mitsinje yamadzi yaphwa, ndi moto wapsereza mabusa a m'chipululu. Muombe lipenga m'Ziyoni, nimufuulitse m'phiri langa lopatulika; onse okhala m'dziko anjenjemere; pakuti tsiku la Yehova lilinkudza, pakuti liyandikira; tsiku la mdima, la mdima wandiweyani, tsiku la mitambo, mitambo yochindikira, ngati m'mbandakucha moyalika pamapiri; mtundu waukulu ndi wamphamvu, panalibe wotere ndi kale lonse, sipadzakhalanso wotere utapita uwu, kufikira zaka za mibadwo yambiri. Moto unyambita pamaso pao, ndi m'mbuyo mwao litentha lawi la moto; kumaso kwao dziko likunga munda wa Edeni, koma m'mbuyo mwao likunga chipululu chopanda kanthu; palibenso wakuwapulumuka. Maonekedwe ao aoneka ngati akavalo, nathamanga ngati akavalo a nkhondo. Atumphako ngati mkokomo wa magaleta pamwamba pa mapiri, ngati kulilima kwa malawi a moto akupsereza ziputu, ngati mtundu wamphamvu wa anthu ondandalikira nkhondo. Pamaso pao mitundu ya anthu ikumva zowawa, nkhope yonse zitumbuluka. Athamanga ngati amphamvu; akwera linga ngati anthu a nkhondo; niliyenda lililonse njira yake, osasokonezeka m'mabande ao. Sakankhana, ayenda lililonse m'mopita mwake; akagwa m'zida, siithyoka nkhondo yao. Alumphira mudzi, athamanga palinga, akwerera nyumba, alowera pamazenera ngati khungu. Dziko lapansi linjenjemera pamaso pao, thambo ligwedezeka, dzuwa ndi mwezi zada, ndi nyenyezi zibweza kuwala kwao; ndipo Yehova amveketsa mau ake pamaso pa khamu lake la nkhondo; pakuti a m'chigono mwake ndi ambirimbiri; pakuti Iye wakuchita mau ake ndiye wamphamvu ndithu; pakuti tsiku la Yehova ndi lalikulu ndi loopsa ndithu; akhoza kupirira nalo ndani? Koma ngakhale tsopano, ati Yehova, munditembenukire Ine ndi mtima wanu wonse, ndi kusala, ndi kulira, ndi kuchita maliro; ndipo ng'ambani mitima yanu, si zovala zanu ai; ndi kutembenukira kwa Yehova Mulungu wanu; pakuti Iye ndiye wachisomo, ndi wodzala chifundo, wosapsa mtima msanga, ndi wochuluka kukoma mtima, ndi woleka choipacho. Kaya, Yona kapena adzabwerera, nadzalekerera, ndi kusiya mdalitso pambuyo pake, ndiwo nsembe yaufa ndi nsembe yothira ya Yehova Mulungu wanu. Ombani lipenga m'Ziyoni, patulani tsiku losala, lalikirani msonkhano woletsa, sonkhanitsani anthu, patulani msonkhano, memezani akuluakulu, sonkhanitsani ana ndi oyamwa mawere; mkwati atuluke m'chipinda mwake, ndi mkwatibwi m'mogona mwake. Ansembe, atumiki a Yehova, alire pakati pa khonde la pakhomo ndi guwa la nsembe, nanene, Alekeni anthu anu, Yehova, musapereka cholowa chanu achitonze, kuti amitundu awalamulire; adzaneneranji mwa anthu, Ali kuti Mulungu wao? Pamenepo Yehova anachitira dziko lake nsanje, nachitira anthu ake chifundo. Ndipo Yehova anayankha, nati kwa anthu ake, Taonani, ndidzakutumizirani tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; ndipo mudzakhuta ndi izo; ndipo sindidzakuperekaninso mukhale chitonzo mwa amitundu; koma ndidzakuchotserani kutali nkhondo ya kumpoto, ndi kulingira kudziko louma ndi lopasuka, a kumaso kwake kunyanja ya kum'mawa, ndi a kumbuyo kwake kunyanja ya kumadzulo; ndi kununkha kwake kudzakwera, ndi fungo lake loipa lidzakwera; pakuti inachita zazikulu. Usaopa, dziko iwe; kondwera, nusekerere; pakuti Yehova wachita zazikulu. Musamaopa, nyama zakuthengo inu; pakuti m'chipululu muphukanso msipu; pakuti mitengo ibala zipatso zao; mikuyu ndi mipesa ipatsa mphamvu zao. Mukondwere tsono, inu ana a Ziyoni, nimusekerere m'Yehova Mulungu wanu; pakuti adzayamba kukupatsani mvula ya chizimalupsa, monga mwa chilungamo chake; nakuvumbitsirani mvula, mvula ya chizimalupsa ndi ya masika mwezi woyamba. Ndipo madwale adzakhala ndi tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; zidzasefuka m'zosungiramo zao. Ndipo ndidzakubwezerani zaka zidazidya dzombe, ndi chirimamine, ndi anoni, ndi chimbalanga, gulu langa lalikulu la nkhondo, limene ndinalitumiza pakati pa inu. Ndipo mudzadyaidya ndi kukhuta, nimudzalemekeza dzina la Yehova Mulungu wanu, amene anachita nanu modabwitsa; ndi anthu anga sadzachita manyazi nthawi zonse. Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndili pakati pa Israele, ndi kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, palibe wina; ndi anthu anga sadzachita manyazi nthawi zonse. Ndipo kudzachitika m'tsogolo mwake, ndidzatsanulira mzimu wanga pa anthu onse, ndi ana aamuna ndi aakazi adzanenera, akuluakulu anu adzalota maloto, anyamata anu adzaona masomphenya; ndi pa akapolo ndi adzakazi omwe ndidzatsanulira mzimu wanga masiku awo. Ndipo ndidzaonetsa zodabwitsa kuthambo ndi pa dziko lapansi, mwazi, ndi moto, ndi utsi tolo. Dzuwa lidzasanduka mdima, ndi mwezi udzasanduka mwazi, lisanadze tsiku la Yehova lalikulu ndi loopsa. Ndipo kudzachitika kuti aliyense adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumutsidwa; pakuti m'phiri la Ziyoni ndi m'Yerusalemu mudzakhala chipulumutso, monga Yehova anatero, ndi mwa otsala amene Yehova adzawaitana. Pakuti taonani, masiku awo, ndi nthawi iyo, pamene ndibwera nao andende a Yuda ndi a Yerusalemu, ndidzasonkhanitsa amitundu onse, ndi kutsikira nao kuchigwa cha Yehosafati; ndipo ndidzaweruzana nao komweko za anthu anga, ndi cholowa changa Israele, amene anawabalalitsa mwa amitundu, nagawa dziko langa. Ndipo anachitira anthu anga maere, napereka mwana wamwamuna kusinthana ndi mkazi wadama, nagula vinyo ndi mwana wamkazi kuti amwe. Ndiponso ndili ndi chiyani ndi inu, Tiro ndi Sidoni, ndi malire onse a Afilisti? Mudzandibwezera chilango kodi? Mukandibwezera chilango msanga, mofulumira, ndidzabwezera chilango chanu pamutu panu. Popeza inu munatenga siliva wanga ndi golide wanga, ndi kulonga zofunika zanga zokoma m'akachisi anu; munagulitsanso ana a Yuda ndi ana a Yerusalemu kwa ana a Yavani, kuwachotsa kutali kwa malire ao; taonani, ndidzawautsa kumalo kumene munawagulitsako, ndi kubwezera chilango chanu pamutu panu; ndipo ndidzagulitsa ana ako aamuna ndi aakazi m'dzanja la ana a Yuda; ndipo iwo adzawagulitsa kwa anthu a Seba, kwa anthu okhala kutali; pakuti Yehova wanena. Mulalikire ichi mwa amitundu, mukonzeretu nkhondo; utsani amuna amphamvu; amuna onse a nkhondo ayandikire nakwere. Sulani makasu anu akhale malupanga, ndi zikwakwa zanu zikhale nthungo; wofooka anene, Ndine wamphamvu. Fulumirani, idzani, amitundu inu nonse pozungulirapo; sonkhanani pamodzi, mutsitsire komweko amphamvu anu, Yehova. Agalamuke amitundu, nakwerere kuchigwa cha Yehosafati; pakuti ndidzakhala komweko kuweruza amitundu onse ozungulira. Longani chisenga, pakuti dzinthu dzacha; idzani, pondani, pakuti chadzala choponderamo mphesa; zosungiramo zisefuka; pakuti zoipa zao nzazikulu. Aunyinji, aunyinji m'chigwa chotsirizira mlandu! Pakuti layandikira tsiku la Yehova m'chigwa chotsirizira mlandu. Dzuwa ndi mwezi zada, ndi nyenyezi zibweza kuwala kwao. Ndipo Yehova adzadzuma ali ku Ziyoni, ndi kumveketsa mau ake ali ku Yerusalemu; ndi thambo ndi dziko lapansi zidzagwedezeka; koma Yehova adzakhala chopulumukirako anthu adzakhala chopulumukirako anthu ake, ndi linga la ana a Israele. Momwemo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu wakukhala m'Ziyoni, phiri langa lopatulika; pamenepo Yerusalemu adzakhala wopatulika, osapitanso alendo pakati pake, Ndipo kudzachitika tsiku ilo mapiri adzakhetsa vinyo wozuna, ndi pazitunda padzayenda mkaka, ndi m'mitsinje yonse ya Yuda mudzayenda madzi; ndi madzi akasupe adzatuluka m'nyumba ya Yehova, nadzamwetsa madzi chigwa cha Sitimu. Ejipito adzasanduka bwinja, ndi Edomu adzasanduka chipululu chopanda kanthu, chifukwa cha chiwawachi anawachitira ana a Yuda; popeza anakhetsa mwazi wosachimwa m'dziko lao. Koma Yuda adzakhala chikhalire, ndi Yerusalemu ku mibadwomibadwo. Ndipo ndidzayeretsa mwazi wao umene sindinauyeretsa, pakuti Yehova akhala m'Ziyoni. Mau a Amosi, amene anali mwa oweta ng'ombe a ku Tekowa, ndiwo amene anawaona za Israele masiku a Uziya mfumu ya Yuda, ndi masiku a Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele, zitatsala zaka ziwiri chisanafike chivomezi. Ndipo anati, Yehova adzadzuma ali m'Ziyoni, nadzamveketsa mau ake ali m'Yerusalemu; podyetsa abusa padzachita chisoni, ndi mutu wa Karimele udzauma. Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Damasiko, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anapuntha Giliyadi ndi zopunthira zachitsulo; koma ndidzatumiza moto kunyumba ya Hazaele, ndipo udzanyeketsa nyumba zachifumu za Benihadadi. Ndipo ndidzathyola mpiringidzo wa Damasiko, ndi kulikha okhala m'chigwa cha Aveni, ndi iye wogwira ndodo yachifumu m'Betedeni; ndi anthu a Aramu adzalowa ndende ku Kiri, ati Yehova. Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Gaza, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anatenga ndende anthu onse kuwapereka kwa Edomu; koma ndidzatumiza moto pa linga la Gaza, ndipo udzatha nyumba zake zachifumu; ndipo ndidzalikha okhala m'Asidodi, ndi iye wogwira ndodo yachifumu m'Asikeloni; ndipo ndidzabwezera Ekeroni dzanja langa limlange; ndi Afilisti otsala adzatayika, ati Ambuye Yehova. Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Tiro, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anapereka anthu onse kwa Edomu, osakumbukira pangano lachibale; koma ndidzatumiza moto pa linga la Tiro, ndipo udzanyeketsa nyumba zake zachifumu. Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Edomu, kapena zinani, sindidzabweza kulanga kwake; popeza analondola mphwake ndi lupanga, nafetsa chifundo chake chonse, ndi mkwiyo wake unang'amba ching'ambire nasunga mkwiyo wake chisungire; koma ndidzatumiza moto pa Temani, udzanyeketsa nyumba zachifumu za Bozira. Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za ana a Amoni, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anatumbula akazi ali m'pakati a Giliyadi, kuti akuze malire ao; koma ndidzayatsa moto pa linga la Raba, udzanyeketsa nyumba zachifumu zake, ndi kufuula tsiku la nkhondo, ndi namondwe, tsiku la kamvulumvulu; ndipo mfumu yao idzalowa kundende, iyo ndi akalonga ake pamodzi, ati Yehova. Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Mowabu, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anatentha mafupa a mfumu ya ku Edomu asanduke njereza; koma ndidzatumiza moto pa Mowabu, udzanyeketsa nyumba zachifumu za Keriyoti; ndipo Mowabu adzafa ndi phokoso, ndi kufuula, ndi mau a lipenga; ndipo ndidzalikha woweruza pakati pake, ndi kupha akalonga ake onse, ati Yehova. Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Yuda, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza akaniza chilamulo cha Yehova, osasunga malemba ake; ndipo awalakwitsa mabodza ao amene makolo ao anawatsata; koma ndidzatumiza moto pa Yuda, udzanyeketsa nyumba zachifumu za m'Yerusalemu. Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Israele, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza agulitsa wolungama ndi ndalama, ndi wosowa chifukwa cha nsapato; ndiwo amene aliralira fumbi lapansi lili pamutu pa wosauka, napotoza njira ya wofatsa; ndipo munthu ndi atate wake amuka kwa namwali yemweyo, kuti aipse dzina langa loyera; nagona pansi pa zofunda za chikole kumaguwa a nsembe ali onse, ndi m'nyumba ya Mulungu wao akumwa vinyo wa iwo olipitsidwa. Koma ndinaononga Ine pamaso pa Aamori, amene msinkhu wao unanga msinkhu wa mikungudza, nakhala nayo mphamvu ngati thundu; koma ndinaononga zipatso zao m'mwamba, ndi mizu yao pansi. Ndipo ndinakukwezani kuchokera m'dziko la Ejipito, ndi kukutsogolerani zaka makumi anai m'chipululu, kuti mulandire dziko la Aamori likhale cholowa chanu. Ndipo ndinaukitsa mwa ana anu aneneri, ndi mwa anyamata anu Anaziri. Si momwemo, inu ana a Israele, ati Yehova? Koma munamwetsa Anaziri vinyo, ndi kulamulira aneneri ndi kuti, Musamanenera. Taonani, ndidzakupsinjani m'malo mwanu, monga lipsinja galeta lodzala ndi mitolo fwa. Ndipo populumukirapo padzasowera waliwiro, ndi wamphamvu; sadzalimbikitsa mphamvu yake, ndi ngwazi siidzapulumutsa moyo wake; ndi wokoka uta sadzalimbika, ndi waliwiro sadzadzipulumutsa; ngakhale woyenda pa akavalo sadzapulumutsa moyo wake; ndi wolimba mtima mwa ngwazi adzathawa wamaliseche tsiku lomwelo, ati Yehova. Tamverani mau awa akunenerani Yehova motsutsa, inu ana a Israele, kulinenera banja lonse ndinalikweza kulitulutsa m'dziko la Ejipito, ndi kuti, Inu nokha ndinakudziwani mwa mabanja onse a pa dziko lapansi, m'mwemo ndidzakulangani chifukwa cha mphulupulu zanu zonse. Kodi awiri adzayenda pamodzi asanapanganiranetu? Kodi mkango udzabangula m'nkhalango wosakhala nayo nyama? Kodi msona wa mkango udzalira m'ngaka mwake usanagwire kanthu? Kodi mbalame idzakodwa mumsampha pansi popanda msampha woitchera? Kodi msampha ufwamphuka pansi wosakola kanthu? Kodi adzaomba lipenga m'mudzi osanjenjemera anthu? Kodi choipa chidzagwera mudzi osachichita Yehova? Pakuti Ambuye Yehova sadzachita kanthu osawulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri. Mkango ukabangula, ndani amene saopa? Ambuye Yehova wanena, ndani amene sanenera? Bukitsani kunyumba zachifumu za Asidodi, ndi kunyumba zachifumu za m'dziko la Ejipito, nimuziti, Sonkhanani pa mapiri a Samariya, ndipo penyani masokosero akulu m'menemo, ndi ozunzika m'kati mwake. Pakuti sadziwa kuchita zolungama, amene akundika zachiwawa ndi umbala m'nyumba zao zachifumu, ati Yehova. Chifukwa chake, atero Ambuye Yehova, Padzakhala mdani pozungulira pake pa dziko, nadzatsitsa kukuchotsera mphamvu yako; ndi za m'nyumba zako zachifumu adzazifunkha. Atero Yehova, Monga mbusa alanditsa m'kamwa mwa mkango miyendo iwiri, kapena kansonga ka khutu, momwemo adzalanditsidwa ana a Israele okhala pansi m'Samariya, m'ngodya ya guwa logonapo, ndi pa mitsamiro ya kama. Tamverani inu, muchitire umboni wotsutsa nyumba ya Yakobo, ati Ambuye Yehova Mulungu wa makamu. Pakuti tsiku lakumlanga Israele chifukwa cha zolakwa zake, ndidzalanganso maguwa a nsembe a ku Betele; ndi nyanga za guwa la nsembe zidzadulidwa, nizidzagwa pansi. Ndipo ndidzakantha nyumba ya nyengo yachisanu, pamodzi ndi nyumba zaminyanga zidzaonongeka; ndi nyumba zazikuluzo zidzatha, ati Yehova. Tamverani mau awa, inu ng'ombe zazikazi za ku Basani, zokhala m'phiri la Samariya, zosautsa aumphawi, zopsinja osowa, zonena kwa ambuyao, Bwerani nacho, timwe. Ambuye Yehova walumbira pali chiyero chake, kuti taonani, adzakugwerani masiku akuti adzakuchotsani ndi zokowera, ndi otsala anu ndi mbedza. Ndipo mudzatulukira popasuka linga, yense m'tsogolo mwake, ndi kutayika ku Harimoni, ati Yehova. Idzani ku Betele, mudzalakwe ku Giligala, nimuchulukitse zolakwa, nimubwere nazo nsembe zanu zophera m'mawa ndi m'mawa, magawo anu akhumi atapita masiku atatuatatu; nimutenthe nsembe zolemekeza zachotupitsa, nimulalikire nsembe zaufulu, ndi kuzimveketsa; pakuti ichi muchikonda, inu ana a Israele, ati Ambuye Yehova. Ndipo Ine ndakupatsaninso mano oyera m'midzi yanu yonse, ndi kusowa mkate m'malo mwanu monse; koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova. Ndipo Ine ndakumanani mvula, itatsala miyezi itatu isanafika nyengo yakukolola; ndipo ndinavumbitsira mudzi umodzi mvula, osavumbitsira mudzi wina; munda wina unavumbidwa mvula, ndi m'munda mosavumbidwa mvula munafota. M'mwemo midzi iwiri kapena itatu inayenda peyupeyu kumudzi umodzi kukamwa madzi, koma sanakhute; koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova. Ndinakukanthani ndi chinsikwi ndi chinoni; minda yanu yochuluka yamipesa, ndi yamikuyu, ndi ya azitona, yaonongeka ndi dzombe; koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova. Ndinatumiza mliri pakati panu monga m'Ejipito; anyamata anu ndawapha ndi lupanga, ndi kutenga akavalo anu; ndipo ndinakweretsa kununkha kwa chigono chanu kufikitsa kumphuno kwanu; koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova. Ndinagubuduza ena mwa inu, monga umo Mulungu anagubuduzira Sodomu ndi Gomora; ndipo inu munali ngati muuni wofumulidwa kumoto; koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova. Chifukwa chake ndidzatero nawe, Israele; popeza ndidzakuchitira ichi, dzikonzeretu kukomana ndi Mulungu wako, Israele. Pakuti taona, Iye amene aumba mapiri, nalenga mphepo, nafotokozera munthu maganizo ake, nasanduliza m'mawa ukhale mdima, naponda pa misanje ya dziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova Mulungu wa makamu. Tamverani mau awa ndinenawa, akhalire inu nyimbo ya maliro, nyumba ya Israele inu. Namwali wa Israele wagwa, sadzaukanso; wagwetsedwa pa nthaka yake, palibe womuutsa. Pakuti atero Ambuye Yehova, M'nyumba ya Israele, mudzi wotulukamo chikwi chimodzi adzautsalira zana limodzi, ndi uwu wotulukamo zana limodzi adzautsalira khumi. Pakuti atero Yehova kwa nyumba ya Israele, Mundifunefune Ine, ndipo mudzakhala ndi moyo; koma musamafuna Betele, kapena kumalowa m'Giligala; musamapita ku Beereseba; pakuti Giligala adzalowadi m'ndende, ndi Betele adzasanduka chabe. Funani Yehova, ndipo mudzakhala ndi moyo; angabuke ngati moto m'nyumba ya Yosefe, ndipo unganyeke wopanda wakuzima m'Betele; inu osintha chiweruzo chikhale chivumulo, nimugwetsa pansi chilungamo. Iye wakulenga Nsangwe ndi Akamwiniatsatana, nasanduliza mdima wandiweyani ukhale m'mawa, nasanduliza usana ude ngati usiku, wakuitana madzi a m'nyanja, nawatsanulira pa dziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova; wakufikitsa chionongeko pa wamphamvu modzidzimuka, chionongeko nichigwera linga. Iwo adana naye wodzudzula kuchipata, nanyansidwa naye wolunjikitsa mau. Popeza tsono mupondereza aumphawi, ndi kumsokhetsa tirigu; mwamanga nyumba za miyala yosema, koma simudzakhala m'mwemo; mwaoka minda ya mipesa yokonda, koma simudzamwa vinyo wake. Pakuti ndidziwa kuti zolakwa zanu nzochuluka, ndi machimo anu ndi olimba, inu akusautsa olungama, akulandira chokometsera mlandu, akukankha osowa kuchipata. Chifukwa chake wochenjerayo akhala chete nthawi yomweyo; pakuti ndiyo nthawi yoipa. Funani chokoma, si choipa ai; kuti mukhale ndi moyo; motero Yehova Mulungu wa makamu adzakhala ndi inu, monga munena. Danani nacho choipa, nimukonde chokoma; nimukhazikitse chiweruzo kuchipata; kapena Yehova Mulungu wa makamu adzachitira chifundo otsala a Yosefe. Chifukwa chake atero Yehova, Mulungu wa makamu, Ambuye, M'makwalala onse mudzakhala kulira, ndi m'miseu yonse adzati, Kalanga ine! Kalanga ine! Nadzaitana wakumunda adze kumaliro, ndi odziwa maliridwe a nthetemya alire. Ndi m'minda yonse yamipesa mudzakhala kulira, pakuti ndipita pakati pako, ati Yehova. Tsoka inu akufuna tsiku la Yehova? Mudzapindulanji nalo tsiku la Yehova? Ndilo mdima, si kuunika ai. Kudzakhala monga munthu akathawa mkango, ndi chimbalangondo chikomana naye; kapena akalowa m'nyumba, natsamira kukhoma ndi dzanja lake, nimluma njoka. Kodi tsiku la Yehova silidzakhala la mdima, si la kuunika ai? Lakuda bii, lopanda kuwala m'menemo? Ndidana nao, ndinyoza zikondwerero zanu, sindidzakondwera nao masonkhano anu oletsa. Inde, mungakhale mupereka kwa Ine nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zaufa, sindidzazilandira Ine; ndi nsembe zoyamika za ng'ombe zanu zonenepa, sindidzazisamalira Ine. Mundichotsere phokoso la nyimbo zanu; sindifuna kumva mayimbidwe a zisakasa zanu. Koma chiweruzo chiyende ngati madzi, ndi chilungamo ngati mtsinje wosefuka. Ngati munabwera nazo kwa Ine nsembe zophera ndi zaufa zaka makumi anai m'chipululu, inu nyumba ya Israele? Inde mwasenza hema wa mfumu yanu, ndi tsinde la mafano anu, nyenyezi ya mulungu wanu, amene mudadzipangira. M'mwemo ndidzakutengani kunka nanu kundende kutsogolo kwa Damasiko, ati Yehova, amene dzina lake ndiye Mulungu wa makamu. Tsoka osalabadirawo m'Ziyoni, ndi iwo okhazikika m'phiri la Samariya, ndiwo anthu omveka a mtundu woposa wa anthu, amene nyumba ya Israele iwafikira! Pitani ku Kaline, nimuone; kuchokera komweko mupite ku Hamati wamkulu mutsikire ku Gati wa Afilisti; kodi awo ndi okoma koposa maufumu ano? Kapena malire ao aposa malire anu? Inu akutalikitsa tsiku loipa, ndi kusendeza pafupi mpando wachiwawa; ogona pamakama aminyanga, nadzithinula pa maguwa ao ogonapo, nadya anaankhosa a kuzoweta, ndi anaang'ombe ochoka pakati pa khola; akungoimba kutsata maliridwe a zeze, nadzilingiririra zoimbira nazo ngati Davide; akumwera vinyo m'zipanda, nadzidzoza ndi mafuta abwino oposa, osagwidwa chisoni ndi kuthyoka kwa Yosefe. Chifukwa chake tsono, adzatengedwa ndende ndi oyamba kutengedwa ndende; ndi phokoso la iwo odzithinula lidzapita. Ambuye Yehova walumbira pali Iye mwini, ati Yehova Mulungu wa makamu, Ndinyansidwa nako kudzikuza kwa Yakobo, ndidana nazo nyumba zake zachifumu; m'mwemo ndidzapereka mudzi, ndi zonse zili m'menemo. Ndipo kudzachitika, mukatsala amuna khumi m'nyumba imodzi, adzafa. Ndipo mbale wake wa munthu akamnyamula, ndiye womtentha, kutulutsa mafupa m'nyumba, nakati kwa iye ali m'kati mwa nyumbamo, Atsala wina nawe kodi? Nakati Iai; pamenepo adzati, Khala chete; pakuti sitingatchule dzina la Yehova. Pakuti taonani, Yehova walamulira, nadzakantha nyumba yaikulu ichite mpata, ndi nyumba yaing'ono ichite mindala. Kodi akavalo adzathamanga pathanthwe? Kodi adzalimako ndi ng'ombe pakuti mwasanduliza chiweruzo chikhale ndulu, ndi chipatso cha chilungamo chikhale chivumulo; inu okondwera nacho chopanda pake, ndi kuti, Kodi sitinadzilimbitsa tokha ndi kulanda Karinaimu mwa mphamvu yathuyathu? Pakuti taonani, ndidzakuutsirani mtundu wa anthu, nyumba ya Israele, ati Yehova Mulungu wa makamu; ndipo adzakupsinjani kuyambira polowera ku Hamati kufikira mtsinje wa kuchidikha. Ambuye Yehova anandionetsa chotere; ndipo taonani, anaumba dzombe, poyamba kuphuka kwa udzu a chibwereza; ndipo taonani, ndicho chibwereza atawasengera mfumu. Ndipo kunachitika m'mene lidatha kudya msipu wa dziko, ndinati, Ambuye Yehova, khululukiranitu Yakobo; adzakhala chilili bwanji? Popeza ndiye wamng'ono. Ndipo Yehova anachileka. Sichidzachitika, ati Yehova. Ambuye Yehova anandionetsa chotere; ndipo taonani, Ambuye Yehova anaitana kuti atsutse ndi moto; ndipo unanyambita chakuya chachikulu ukadanyambitanso dziko. Pamenepo ndinati, Ambuye Yehova, lekanitu; Yakobo adzakhala chilili bwanji? Pakuti ali wamng'ono. Ndipo Yehova anachileka. Ichi chomwe sichidzachitika, ati Ambuye Yehova. Anandionetsa chotere; ndipo taonani, Ambuye anaima pa khoma lomangidwa ndi chingwe cholungamitsira chilili; ndi chingwe cholungamitsira chilili m'dzanja lake. Ndipo Yehova anati kwa ine, Amosi, uona chiyani? Ndipo ndinati, Chingwe cholungamitsira chilili. Nati Ambuye, Taona, ndidzaika chingwe cholungamitsira chilili pakati pa anthu anga Israele, sindidzawalekanso: ndi misanje ya Isaki idzakhala bwinja; ndi malo opatulika a Israele adzapasuka; ndipo ndidzaukira nyumba ya Yerobowamu ndi lupanga. Pamenepo Amaziya wansembe wa ku Betele anatumiza kwa Yerobowamu mfumu ya Israele, ndi kuti, Amosi wapangira inu chiwembu pakati pa nyumba ya Israele; dziko silikhoza kulola mau ake onse. Pakuti atero Amosi, Yerobowamu adzafa ndi lupanga, ndi Israele adzatengedwadi ndende, kuchoka m'dziko lake. Amaziya anatinso kwa Amosi, Mlauli iwe, choka, thawira kudziko la Yuda, nudye, nunenere komweko; koma usaneneranso ku Betele; pakuti pamenepo mpa malo opatulika a mfumu, ndiyo nyumba yachifumu. Pamenepo Amosi anayankha, nati kwa Amaziya, Sindinali mneneri, kapena mwana wa mneneri, koma ndinali woweta ng'ombe, ndi wakutchera nkhuyu; ndipo Yehova ananditenga ndilikutsata nkhosa, nati kwa ine Yehova, Muka, nenera kwa anthu anga Israele. Chifukwa chake tsono, tamvera mau a Yehova, Iwe ukuti, Usamanenera chotsutsana ndi Israele, usadonthetsa mau akutsutsana ndi nyumba ya Isaki; chifukwa chake atero Yehova, Mkazi wako adzakhala wadama m'mudzi, ndi ana ako aamuna ndi aakazi adzagwa ndi lupanga, ndi dziko lako lidzagawanidwa ndi kuyesa chingwe, ndi iwe mwini udzafa m'dziko lodetsedwa; ndipo Israele adzatengedwadi ndende kuchoka m'dziko lake. Ambuye Yehova anandionetsa chotere; ndipo taonani, dengu la zipatso zamalimwe. Ndipo anati, Amosi uona chiyani? Ndipo ndinati, Dengu la zipatso zamalimwe. Nati Yehova kwa ine, Chitsiriziro chafikira anthu anga Israele, sindidzawalekanso. Koma nyimbo za ku Kachisi zidzasanduka kubuma tsiku ilo, ati Ambuye Yehova; mitembo idzachuluka; adzaitaya paliponse padzakhala zii. Tamverani ichi, inu akumeza aumphawi, ndi kuwatha ofatsa m'dziko, ndi kuti, Mwezi wokhala upita liti, kuti tigulitse dzinthu? Ndi Sabata, kuti titsegulire tirigu? Ndi kuchepsa efa, ndi kukulitsa sekeli, ndi kuchenjerera nayo miyeso yonyenga; kuti tigule osauka ndi ndalama, ndi aumphawi ndi nsapato, ndi kugulitsa nsadwa za tirigu. Yehova walumbira pali kudzikuza kwa Yakobo, Ngati ndidzaiwala konse ntchito zao zilizonse? Kodi dziko silidzanjenjemera chifukwa cha ichi, ndi kulira aliyense wokhalamo? Inde lidzakwera lonseli ngati madzi a m'mtsinje; lidzagwezeka, ndi kutsikanso ngati mtsinje wa Ejipito. Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ati Ambuye Yehova, ndidzalowetsa dzuwa usana, ndi kudetsa dziko pausana poyera. Ndipo ndidzasanduliza zikondwerero zanu zikhale maliro, ndi nyimbo zanu zikhale za maliro, ndi kufikitsa ziguduli m'chuuno monse, ndi mpala pa mutu uliwonse; nadzakhala ngati maliro a mwana mmodzi yekha, ndi chitsiriziro chake ngati tsiku lowawa. Taonani, akudza masiku, ati Ambuye Yehova, akuti ndidzatumiza njala m'dzikomo, si njala ya mkate kapena ludzu la madzi, koma njala ya kumva mau a Yehova. Ndipo adzayendayenda peyupeyu kuyambira kunyanja kufikira kunyanja ndi kuyambira kumpoto kufikira kum'mawa; adzathamangathamanga kufunafuna mau a Yehova, koma osawapeza. Tsiku lomwelo anamwali okongola ndi anyamata adzakomoka nalo ludzu. Iwo akulumbira ndi kutchula tchimo la Samariya, ndi kuti, Pali Mulungu wako, Dani; ndipo, Pali moyo wa njira ya ku Beereseba, iwowa adzagwa, osaukanso konse. Ndinaona Ambuye alikuima pa guwa la nsembe, nati Iye, Kantha mitu ya nsanamira, kuti ziundo zigwedezeke; nuphwanye mitu yao yonse; ndipo ndidzapha otsiriza ao ndi lupanga; wothawayo mwa iwo sadzathawadi, ndi wopulumukayo mwa iwo sadzapulumukadi. Angakhale akumba mpaka kunsi kwa manda, dzanja langa lidzawatenga kumeneko; angakhale akwera kumwamba, ndidzawatsitsa komweko. Angakhale abisala pamwamba pa Karimele, ndidzawapwaira ndi kuwatenga komweko; angakhale abisala pamaso panga pansi pa nyanja, kumeneko ndidzalamulira njoka, ndipo idzawaluma. Angakhale alowa ndende pamaso pa adani ao, kumeneko ndidzalamulira lupanga, ndipo lidzawapha; ndipo ndidzayang'anitsa maso anga kwa iwowa, kuwachitira choipa, si chokoma ai. Pakuti Ambuye Yehova wa makamu ndiye amene akhudza dziko, nilisungunuka; ndi onse okhalamo adzachita maliro; ndipo lidzakwera lonseli ngati madzi a m'nyanja; nilidzatsikanso ngati nyanja ya m'Ejipito; ndiye amene amanga zipinda zake zosanja m'mwamba, nakhazika tsindwi lake pa dziko lapansi; Iye amene aitana madzi a m'nyanja, nawatsanulira padziko; dzina lake ndiye Yehova. Kodi simukhala kwa Ine ngati ana a Kusi, inu ana a Israele? Ati Yehova. Sindinakweza Israele ndine, kumtulutsa m'dziko la Ejipito, ndi Afilisti ku Kafitori, ndi Aaramu ku Kiri? Taonani, maso a Ambuye Yehova ali pa ufumu wochimwawo, ndipo ndidzauononga kuuchotsa pa dziko lapansi; pokhapo sindidzaononga nyumba ya Yakobo kuitha konse, ati Yehova. Pakuti taonani, ndidzalamulira, ndipo ndidzapeta nyumba ya Israele mwa amitundu onse, monga apeta tirigu m'lichero; koma silidzagwa pansi diso, ndi limodzi lonse. Ochimwa onse a anthu anga adzafa ndi lupanga, ndiwo amene akuti, Choipa sichidzatipeza, kapena kutidulira. Tsiku lomwelo ndidzautsa msasa wa Davide udagwawo, ndi kukonzanso zopasuka zake; ndipo ndidzautsa zogumuka zake, ndi kuumanga monga masiku a kalelo; kuti alandire otsala a Edomu akhale cholowa chao, ndi amitundu onse a kutchedwa dzina langa, ati Yehova wakuchita izi. Taonani, akudza masiku, ati Yehova, akuti wolima adzapezana ndi wodula, ndi woponda mphesa adzapezana ndi wofetsa, ndi mapiri adzakhetsa vinyo watsopano, ndi zitunda zonse zidzasungunuka. Ndipo ndidzabwezanso undende wa anthu anga Israele, ndipo adzamanganso mabwinja, ndi kukhala m'menemo; nadzaoka minda ya mipesa nadzamwa vinyo wake, nadzalima minda ndi kudya zipatso zake. Ndipo ndidzawaoka m'dziko mwao ndipo sadzazulidwanso m'dziko lao limene ndawapatsa, ati Yehova Mulungu wako. Masomphenya a Obadiya. Atero Ambuye Yehova za Edomu: Tamva mbiri yochokera kwa Yehova, ndi mthenga wotumidwa mwa amitundu, ndi kuti, Nyamukani, timuukire kumthira nkhondo. Taona, ndakuika wamng'ono mwa amitundu; unyozedwa kwambiri. Kudzikuza kwa mtima wako kwakunyenga, iwe wokhala m'mapanga a thanthwe, iwe pokhala pako pamwamba, wakunena m'mtima mwake, Adzanditsitsira pansi ndani? Chinkana ukwera pamwamba penipeni ngati chiombankhanga, chinkana chisanja chako chisanjika pakati pa nyenyezi, ndidzakutsitsa kumeneko, ati Yehova. Akakudzera akuba, kapena mbala usiku, (Ha! Waonongeka) sadzaba mpaka adzakhuta kodi? Akakudzera akutchera mphesa sadzasiya khunkha kodi? Ha! Za Esau zasanthulidwa; ha! Zobisika zake zafunidwa. Anthu onse a akupangana nawe anakuperekeza mpaka pamalire; anthu okhala ndi mtendere nawe anakunyenga, nakuposa mphamvu; iwo akudya chakudya chako akutchera msampha pansi pako; mulibe nzeru mwa iye. Ati Yehova, Kodi sindidzaononga tsiku lija anzeru mwa Edomu, ndi luntha m'phiri la Esau? Ndipo amuna anu amphamvu adzatenga nkhawa, Temani iwe, kuti onse aonongeke m'phiri la Edomu, ndi kuphedwa. Chifukwa cha chiwawa unamchitira mphwako Yakobo, udzakutidwa ndi manyazi, nudzaonongeka kunthawi yonse. Tsiku lija unaima padera, tsiku lija alendo anagwira ndende makamu ake, nalowa m'zipata zake achilendo, nachitira Yerusalemu maere, iwenso unakhala ngati mmodzi wa iwowa. Koma usapenyerera tsiku la mphwako, tsiku loyesedwa mlendo iye, nusasekerere ana a Yuda tsiku la kuonongeka kwao, kapena kuseka chikhakha tsiku lakupsinjika. Usalowe m'mudzi wa anthu anga tsiku la tsoka lao, kapena kupenyerera iwe choipa chao tsiku la tsoka lao, kapena kuthira manja khamu lao tsiku la tsoka lao. Ndipo usaime pamphambano kuononga opulumuka ake; kapena kupereka otsala ake tsiku lakupsinjika. Pakuti tsiku la Yehova layandikira amitundu onse; monga unachita iwe, momwemo adzakuchitira; chochita iwe chidzakubwerera pamtu pako. Pakuti monga munamwa pa phiri langa lopatulika, momwemo amitundu onse adzamwa kosalekeza; inde adzamwa, nadzameza, nadzakhala monga ngati sanalipo. Koma m'phiri la Ziyoni mudzakhala opulumuka, ndipo lidzakhala lopatulika; ndi a nyumba ya Yakobo adzakhala nazo zolowa zao. Ndipo nyumba ya Yakobo idzakhala moto, ndi nyumba ya Yosefe lawi, ndi nyumba ya Esau ngati chiputu, ndipo adzawatentha pakati pao, ndi kuwapsereza; ndipo sadzakhalapo otsalira nyumba ya Esau; pakuti Yehova wanena. Ndipo akumwera adzakhala nalo phiri la Esau cholowa chao; ndi iwo a kuchidikha adzakhala nalo dziko la Afilisti; ndipo adzakhala nayo minda ya Efuremu, ndi minda ya Samariya cholowa chao; ndi Benjamini adzakhala nalo la Giliyadi. Ndipo andende a khamu ili la ana a Israele, okhala mwa Akanani, adzakhala nacho cholowa chao mpaka pa Zarefati; ndi andende a ku Yerusalemu okhala m'Sefaradi adzakhala nayo midzi ya kumwera, cholowa chao. Ndipo apulumutsi adzakwera pa phiri la Ziyoni kuweruza phiri la Esau; ndipo ufumu udzakhala wake wa Yehova. Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yona mwana wa Amitai, ndi kuti, Nyamuka, pita ku Ninive, mudzi waukuluwo, nulalikire motsutsana nao; pakuti choipa chao chandikwerera pamaso panga. Koma Yona ananyamuka kuti athawire ku Tarisisi, kuzemba Yehova; ndipo anatsikira ku Yopa, napezako chombo chomuka ku Tarisisi, napereka ndalama zake, natsikira m'menemo, kuti apite nao ku Tarisisi kuzemba Yehova. Koma Yehova anautsa chimphepo chachikulu panyanja, ndipo panali namondwe wamkulu panyanja, ndi chombo chikadasweka. Pamenepo amalinyero anachita mantha, nafuulira yense kwa mulungu wake, naponya m'nyanja akatundu anali m'chombo kuchipepuza. Koma Yona adatsikira m'munsi mwa chombo, nagona tulo tofa nato. Ndipo mwini chombo anadza kwa iye, nanena naye, Utani iwe wam'tulo? Uka, itana Mulungu wako, kapena Mulunguyo adzatikumbukira tingatayike. Ndipo anati yense kwa mnzake, Tiyeni tichite maere, kuti tidziwe choipa ichi chatigwera chifukwa cha yani. M'mwemo anachita maere, ndipo maere anagwera Yona. Pamenepo anati kwa iye, Utiuzetu choipa ichi chatigwera chifukwa cha yani? Ntchito yako njotani? Ufumu kuti? Dziko lako nliti? Nanga mtundu wako? Ndipo ananena nao, Ndine Muhebri, ndiopa Yehova Mulungu wa Kumwamba, amene analenga nyanja ndi mtunda. Pamenepo amunawo anaopa kwambiri, nati kwa iye, Ichi nchiyani wachichita? Pakuti amunawo anadziwa kuti anathawa pamaso pa Yehova, popeza adawauza. Tsono anati kwa iye, Tichitenji nawe, kuti nyanja itichitire bata? Popeza namondwe anakulakulabe panyanja. Ndipo anati nao, Mundinyamule ndi kundiponya m'nyanja, momwemo nyanja idzachitira inu bata; pakuti ndidziwa kuti namondwe wamkulu amene wakugwerani chifukwa cha ine. Koma amunawo anapalasa kubwerera kumtunda, koma sanathe; pakuti namondwe wa panyanja anakulakula mokomana nao. Pamenepo anafuulira kwa Yehova, nati, Tikupemphanitu, Yehova, tisatayike chifukwa cha moyo wa munthu uyu, musatisenzetse mwazi wosachimwa; pakuti, Inu Yehova, mwachita monga mudakomera Inu. Momwemo ananyamula Yona, namponya m'nyanja; ndipo nyanja inaleka kukokoma kwake. Ndipo amunawo anaopa Yehova ndi mantha akulu, namphera Yehova nsembe, nawinda. Koma Yehova anaikiratu chinsomba chachikulu chimeze Yona; ndipo Yona anali m'mimba mwa nsombayi masiku atatu usana ndi usiku. Pamenepo Yona anapemphera kwa Yehova Mulungu wake ali m'mimba mwa nsombayo. Ndipo anati, Ndinaitana Yehova m'nsautso yanga, ndipo anandiyankha ine; ndinafuula ndili m'mimba ya manda, ndipo munamva mau anga. Pakuti munandiponya mwakuya m'kati mwa nyanja, ndipo madzi anandizinga; mafunde anu onse a nyondonyondo anandimiza. Ndipo ndinati, Ndatayika ndichoke pamaso panu; koma ndidzapenyanso Kachisi wanu wopatulika. Madzi anandizinga mpaka moyo wanga, madzi akuya anandizungulira, kayandeyande wa m'nyanja anandikulunga mutu. Ndinatsikira kumatsinde a mapiri, mipingiridzo ya dziko inanditsekereza kosatha; koma munandikwezera moyo wanga kuuchotsa kuchionongeko, Yehova Mulungu wanga. Pokomoka moyo wanga m'kati mwanga ndinakumbukira Yehova; ndi pemphero langa linafikira Inu m'Kachisi wanu wopatulika. Iwo osamalira mabodza opanda pake ataya chifundo chaochao. Koma ine ndidzakupherani Inu nsembe ndi mau akuyamika, ndidzakwaniritsa chowinda changa. Chipulumutso ncha Yehova. Pamenepo Yehova analankhula ndi nsombayo, ndipo inamsanzira Yona kumtunda. Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yona nthawi yachiwiri, ndi kuti, Nyamuka, pita ku Ninive mudzi waukulu uja, nuulalikire uthenga umene ndikuuza. Ndipo Yona ananyamuka, napita ku Ninive, monga mwa mau a Yehova. Koma Ninive ndiwo mudzi waukulu pamaso pa Yehova, wa ulendo wa masiku atatu. Ndipo Yona anayamba kulowa mudziwo ulendo wa tsiku limodzi, nalalikira, nati, Atsala masiku makumi anai ndipo Ninive adzapasuka. Ndipo anthu a Ninive anakhulupirira Mulungu, nalalikira chosala, navala chiguduli, kuyambira wamkulu kufikira wamng'ono wa iwowa. Pakuti mau awa anafikira mfumu ya Ninive, ndipo inanyamuka kumpando wake wachifumu, nivula chofunda chake, nifunda chiguduli, nikhala m'maphulusa. Ndipo analalikira, nanena m'Ninive mwa lamulo la mfumu ndi nduna zake, ndi kuti, Ngakhale munthu kapena nyama, ngakhale ng'ombe kapena nkhosa, zisalawe kanthu, zisadye, zisamwe madzi; koma zifundidwe ndi chiguduli munthu ndi nyama, nizifuulire kolimba kwa Mulungu; ndipo abwere yense kuleka njira yake yoipa, ndi chiwawa chili m'manja mwake. Kaya, akatembenuka Mulungu, ndi kuleka kubwera ku mkwiyo wake waukali, kuti tisatayike. Ndipo Mulungu anaona ntchito zao, kuti anabwera kuleka njira yao yoipa; ndipo Mulungu analeka choipa adanenachi kuti adzawachitira, osachichita. Koma sikudakomera Yona konse, ndipo anapsa mtima. Ndipo anapemphera kwa Yehova, nati, Ha, Yehova! Si ndiwo mau anga ndikali m'dziko langa? Chifukwa chake ndinafulumira kuthawira ku Tarisisi, pakuti ndinadziwa kuti Inu ndinu Mulungu wachisomo ndi wodzala chifundo, wolekerera ndi wokoma mtima mochuluka, ndi woleka choipacho. Ndipo tsopano, Yehova, mundichotseretu moyo wanga, kundikomera ine kufa, osakhala ndi moyo ai. Ndipo Yehova anati, Uyenera kupsa mtima kodi? Pamenepo Yona anatuluka m'mudzi, nakhala pansi kum'mawa kwa mudzi, nadzimangira komweko thandala, nakhala pansi pake mumthunzi mpaka adzaona chochitikira mudzi. Ndipo Yehova Mulungu anaikiratu msatsi, naumeretsera Yona, uchite mthunzi pamutu pake, kumlanditsa m'nsautso yake. Ndipo Yona anakondwera kwambiri chifukwa cha msatsiwo. Koma Mulungu anauikira mphanzi pakucha m'mawa mwake, ndiyo inadya msatsi, nufota. Ndipo kunali, potuluka dzuwa Mulungu anaika mphepo ya kum'mawa yotentha, ndipo dzuwa linatentha mutu wake wa Yona, nalefuka iye, nadzipempherera kuti afe; nati, Kundikomera ine kufa, kukhala ndi moyo ai. Ndipo Mulungu anati kwa Yona, Uyenera kodi kupsa mtima chifukwa cha msatsiwo? Nati iye, Ee, kundiyenera ine kupsa mtima mpaka imfa. Ndipo Yehova anati, Unachitira chifundo msatsiwo umene sunagwirapo ntchito, kapena kuumeretsa, umene unamera usiku, nutha usiku; ndipo sindiyenera Ine kodi kuchitira chifundo Ninive mudzi waukulu uwu; m'mene muli anthu oposa zikwi zana limodzi mphambu zikwi makumi awiri osadziwa kusiyanitsa pakati pa dzanja lao lamanja ndi lamanzere, ndi zoweta zambiri zomwe? Mau a Yehova amene anadza kwa Mika wa ku Moreseti masiku a Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda, amene adaona za Samariya ndi Yerusalemu. Imvani, mitundu ya anthu, inu nonse; tamvera, dziko lapansi, ndi zonse zili m'mwemo; ndipo Ambuye Yehova akhale mboni yakutsutsa inu, Ambuye m'Kachisi wake wopatulika. Pakuti, taonani, Yehova alikutuluka m'malo mwake, nadzatsika, nadzaponda pa misanje ya dziko lapansi. Ndi mapiri adzasungunuka pansi pa Iye, ndi zigwa zidzang'ambika, ngati sera pamoto, ngati madzi otsanulidwa potsetseremba. Chichitika ichi chonse chifukwa cha kulakwa kwa Yakobo, ndi machimo a nyumba ya Israele. Kulakwa kwa Yakobo nkotani? Si ndiko Samariya? Ndi misanje ya Yuda ndi iti? Si ndiyo Yerusalemu? Chifukwa chake ndidzaika Samariya ngati mulu wa miyala ya m'munda, ngati zooka m'munda wamphesa; ndipo ndidzataya miyala yake m'chigwa, ndi kufukula maziko ake. Ndi mafano ake osema onse adzaphwanyika, ndi mphotho zake zonse zidzatenthedwa ndi moto, ndi mafano ake onse ndidzawapasula; pakuti anazisonkhanitsa pa mphotho ya mkazi wachiwerewere, ndipo zidzabwerera kumphotho ya mkazi wachiwerewere. Chifukwa cha ichi ndidzachita maliro, ndi kuchema, ndidzayenda wolandidwa ndi wamaliseche; ndidzalira ngati nkhandwe, ndi kubuma ngati nthiwatiwa. Pakuti mabala ake ndi osapola; pakuti afikira ku Yuda; afikira ku chipata cha anthu anga, ku Yerusalemu. Musachifotokoza m'Gati, musalira misozi konse; m'nyumba ya Afira ndinagubuduka m'fumbi. Pitiratu, wokhala m'Safiri iwe, wamaliseche ndi wamanyazi; wokhala m'Zanani sanatuluke; maliro a Betezele adzakulandani pokhala pake. Pakuti wokhala m'Maroti alindira chokoma, popeza choipa chatsika kwa Yehova kunka kuchipata cha Yerusalemu. Manga galeta kukavalo waliwiro, wokhala m'Lakisi iwe, woyamba kuchimwitsa mwana wamkazi wa Ziyoni ndi iye; pakuti zolakwa za Israele zinapezedwa mwa iwe. Chifukwa chake pereka mphatso zolawirana kwa Moreseti-Gati; nyumba za Akizibu zidzakhala chinthu chabodza kwa mafumu a Israele. Ndidzakutengeranso wokhala m'Maresa iwe, iye amene adzakulandira ukhale cholowa chake; ulemerero wa Israele udzafikira ku Adulamu. Udziyeseze wadazi, udzimete wekha chifukwa cha ana ako okondwera nao; kuza dazi lako ngati la muimba; pakuti anakuchokera, nalowa ndende. Tsoka iwo akulingirira chinyengo, ndi kukonza choipa pakama pao! Kutacha m'mawa achichita, popeza chikhozeka m'manja mwao. Ndipo akhumbira minda, nailanda; ngakhale nyumba, nazichotsa; asautsa mwamuna ndi nyumba yake, inde munthu ndi cholowa chake. Chifukwa chake atero Yehova, Taonani, ndilingirira choipa pa banja ili, chimene simudzachotsako makosi anu, kapena kuyenda modzikuza inu; pakuti nyengo iyi ndi yoipa. Tsiku ilo adzanena fanizo lakunena inu, nadzalira maliro olemerera, ndi kuti, Tapasuka konse; iye asintha gawo la anthu anga; ha! Andichotsera ili! Agawira opikisana minda yathu. Chifukwa chake udzasowa woponya chingwe chamaere m'msonkhano wa Yehova. Musamanenera, amanenera ati. Sadzanenera kwa awa; matonzo sadzachoka. Kodi adzati, Nyumba ya Yakobo iwe, Mzimu wa Yehova waperewera kodi? Izi ndi ntchito zake kodi? Mau anga samchitira zokoma kodi, iye amene ayenda choongoka? Koma ngakhale dzulo anthu anga anauka ngati mdani; mukwatula chofunda kumalaya a iwo opitirira mosatekeseka, ngati anthu osafuna nkhondo. Muwataya akazi a anthu anga kunja kwa nyumba zao zokondweretsa; muchotsa ulemerero wanga kwa ana ao kosatha. Nyamukani, chokani, pakuti popumula panu si pano ai; chifukwa cha udyo wakuononga ndi chionongeko chachikulu. Munthu akayenda ndi mtima wachinyengo ndi kunama, ndi kuti, Ndidzanenera kwa iwe za vinyo ndi chakumwa chakuledzeretsa; iye ndiye mneneri wa anthu ake. Ndidzakumemezani ndithu, Yakobo, inu nonse; ndidzasonkhanitsa ndithu otsala a Israele; ndidzawaika pamodzi ngati nkhosa za ku Bozira; ngati zoweta pakati pa busa pao adzachita phokoso chifukwa cha kuchuluka anthu. Wothyola wakwera pamaso pao; iwo anathyola, napita kuchipata, natuluka pomwepo; ndi mfumu yao yapita pamaso pao, ndipo Yehova awatsogolera. Ndipo ndinati, Imvanitu, inu akulu a Yakobo, ndi oweruza a nyumba ya Israele; simuyenera kodi kudziwa chiweruzo? Inu amene mudana nacho chokoma ndi kukondana nacho choipa; inu akumyula khungu lao pathupi pao, ndi mnofu wao pa mafupa ao; inu amene mukudyanso mnofu wa anthu anga; ndi kusenda khungu lao ndi kuthyola mafupa ao; inde awaduladula ngati nyama yoti aphike, ndi ngati nyama ya mumphika. Pamenepo adzafuulira kwa Yehova, koma sadzawayankha; inde, adzawabisira nkhope yake nthawi yomweyo, monga momwe anaipsa machitidwe ao. Atero Yehova za aneneri akulakwitsa anthu anga; akuluma ndi mano ao, ndi kufuula, Mtendere; ndipo aliyense wosapereka m'kamwa mwao, amkonzera nkhondo; chifukwa chake kudzakhala ngati usiku kwa inu, wopanda masomphenya; ndipo kudzadera inu, wopanda kulosa; ndi dzuwa lidzalowera aneneri, ndi usana udzawadera bii. Ndipo alauli adzachita manyazi, ndi olosa adzathedwa nzeru; ndipo onsewo adzasunama; pakuti kuyankha kwa Mulungu kulibe. Koma ine ndidzala nayo mphamvu mwa Mzimu ya Yehova, ndi chiweruzo, ndi chamuna, kufotokozera Yakobo kulakwa kwake, ndi kwa Israele tchimo lake. Tamvanitu ichi, akulu a nyumba ya Yakobo inu, ndi oweruza a nyumba ya Israele inu, akuipidwa nacho chiweruzo, ndi kupotoza zoongoka zonse. Amanga Ziyoni ndi mwazi, ndi Yerusalemu ndi chisalungamo. Akulu ake aweruza chifukwa cha mphotho, ndi ansembe ake aphunzitsa chifukwa cha malipo, ndi aneneri ake alosa chifukwa cha ndalama; koma atsamira pa Yehova, nati, Kodi Yehova sali pakati pa ife? Palibe choipa chodzatigwera. Momwemo Ziyoni adzalimidwa ngati munda chifukwa cha inu, ndi m'Yerusalemu mudzasanduka miunda, ndi phiri la nyumba ngati misanje ya m'nkhalango. Koma kudzachitika masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pamwamba pa mapiri, nilidzakuzika pamwamba pa zitunda; ndi mitundu ya anthu idzayendako. Ndipo amitundu ambiri adzamuka, nadzati, Tiyeni, tikwere kuphiri la Yehova, ndi kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; kuti Iye atiphunzitse njira zake, ndipo tidzayenda m'mabande ake; pakuti ku Ziyoni kudzatuluka chilamulo, ndi ku Yerusalemu mau a Yehova. Ndipo Iye adzaweruza mwa mitundu yambiri ya anthu, nadzadzudzula amitundu amphamvu ali kutali; ndipo iwo adzasula malupanga ao akhale makasu, ndi mikondo yao ikhale zolimira, mtundu wa anthu sudzasamulira mtundu unzake lupanga, kapena kuphunziranso nkhondo. Koma adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena. Pakuti mitundu yonse ya anthu idzayenda, wonse m'dzina la mulungu wake, ndipo ife tidzayenda m'dzina la Yehova Mulungu wathu kunthawi yonka muyaya. Tsiku ilo, ati Yehova, ndidzamemeza wakutsimphinayo, ndi kusonkhanitsa wopirikitsidwayo, ndi iye amene ndinamsautsa; ndipo wotsimphinayo ndidzamuyesa wotsala, ndi iye wotayidwa kutali mtundu wamphamvu; ndipo Yehova adzakhala mfumu yao m'phiri la Ziyoni kuyambira pamenepo kufikira kosatha. Ndipo iwe, nsanja ya nkhosa, chitunda cha mwana wamkazi wa Ziyoni, udzafikira iwe, inde udzafika ulamuliro wakale, ufumu wa mwana wamkazi wa Yerusalemu. Tsono ufuulitsa chifukwa ninji? Palibe mfumu mwa iwe kodi? Watayika kodi mu uphungu wako, kuti zowawa zakugwira ngati mkazi wobala? Imva zowawa, nuyesetse kubala, mwana wamkazi wa Ziyoni, ngati mkazi wakubala; pakuti udzatuluka m'mudzi tsopano, nudzakhala kuthengo, nudzafika ku Babiloni; komweko udzapulumutsidwa; komweko Yehova adzakuombola m'manja a adani ako. Ndipo tsopano amitundu ambiri asonkhana kuyambana nawe, akuti, Aipsidwe, diso lathu lipenye ku Ziyoni. Koma sadziwa zolingirira za Yehova, kapena kuzindikira uphungu wake; pakuti anawasonkhanitsa ngati mitolo kudwale. Nyamuka nupunthe, mwana wamkazi wa Ziyoni; pakuti ndidzasanduliza nyanga yako ikhale yachitsulo, ndi ziboda zako zikhale zamkuwa; ndipo udzaphwanya mitundu yambiri ya anthu; ndipo uzipereka chiperekere phindu lao kwa Yehova, ndi chuma chao kwa Ambuye wa dziko lonse lapansi. Uzisonkhana tsopano magulumagulu, mwana wamkazi wa magulu iwe; watimangira misasa, adzapanda woweruza wa Israele ndi ndodo patsaya. Koma iwe, Betelehemu Efurata, ndiwe wamng'ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditulukira wina wakudzakhala woweruza m'Israele; matulukiro ake ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba. Chifukwa chake Iye adzawapereka kufikira nthawi yoti wobalayo wabala; pamenepo otsala a abale ake adzabwera pamodzi ndi ana a Israele. Ndipo adzaimirira, nadzadyetsa nkhosa zake mu mphamvu ya Yehova, m'ukulu wa dzina la Yehova Mulungu wake; ndipo iwo adzakhalabe; pakuti pamenepo Iye adzakhala wamkulu kufikira malekezero a dziko lapansi. Ndipo ameneyo adzakhala Mtendere; pamene a ku Asiriya adzalowa m'dziko lathu, ndi pamene adzaponda m'zinyumba zathu, tidzawaukitsira abusa asanu ndi awiri, ndi akalonga asanu ndi atatu. Ndipo iwo adzatha dziko la Asiriya ndi lupanga, ndi dziko la Nimirodi, ndilo polowera pake; ndipo adzatilanditsa kwa a ku Asiriya pamene alowa m'dziko lathu, pamene aponda m'kati mwa malire athu. Ndipo otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mame ochokera kwa Yehova ngati mvula paudzu, yosachedwera munthu, yosalindira ana a anthu. Ndipo otsala a Yakobo adzakhala mwa amitundu, pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mkango mwa nyama zakuthengo, ngati msona wa mkango mwa magulu a nkhosa; umenewo ukapitako, upondereza, numwetula, ndipo palibe wakupulumutsa. Dzanja lako likwezeke pamwamba pa iwo akuyambana nawe, ndi adani ako onse aonongeke. Ndipo kudzachitika tsiku ilo, ati Yehova, ndidzaononga akavalo ako m'kati mwako, ndi kutha magaleta ako; ndipo ndidzaononga midzi ya m'dziko lako, ndi kupasula malinga ako onse; ndipo ndidzaononga zanyanga za m'dzanja lako; ndipo sudzakhalanso nao alosi; ndidzaononganso mafano ako osema, ndi zoimiritsa zako pakati pako; ndipo sudzalambiranso ntchito za manja ako. Ndipo ndidzazula zifanizo zako m'kati mwako, ndi kutha midzi yako. Ndipo ndidzabwezera amitundu osamvera chilango mu mkwiyo waukali. Tamverani tsono chonena Yehova: Nyamuka, tsutsana nao mapiri, ndi zitunda zimve mau ako. Tamverani, mapiri inu, chitsutsano cha Yehova, ndi inu maziko olimba a dziko lapansi; pakuti Yehova ali nacho chitsutsano ndi anthu ake, ndipo adzatsutsana ndi Israele. Anthu anga inu, ndakuchitirani chiyani? Ndakulemetsani ndi chiyani? Chitani umboni wonditsutsa. Pakuti ndinakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito, ndi kuombola inu m'nyumba ya ukapolo; ndipo ndinatuma akutsogolereni Mose, Aroni, ndi Miriyamu. Anthu anga, kumbukiranitu chofunsira Balaki mfumu ya Mowabu, ndi chomuyankha Balamu mwana wa Beori, kuyambira ku Sitimu kufikira ku Giligala; kuti mudziwe zolungama za Yehova. Ndidzafika kwa Yehova ndi chinai, ndi kuwerama kwa Mulungu Wam'mwamba? Kodi ndifike kwa Iye ndi nsembe zopsereza, ndi anaang'ombe a chaka chimodzi? Kodi Yehova adzakondwera nazo nkhosa zamphongo zikwi, kapena ndi mitsinje ya mafuta zikwi khumi? Kodi ndipereke mwana wanga woyamba chifukwa cha kulakwa kwanga, chipatso cha thupi langa chifukwa cha kuchimwa kwa moyo wanga? Iye anakuuza, munthuwe, chomwe chili chokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako. Mau a Yehova aitana mudzi, ndi wanzeru aopa dzina lanu; tamverani ndodo, ndi Iye amene anaiika. Kodi m'nyumba ya woipa mukali chuma chosalungama, ndi muyeso wochepa umene ayenera kuipidwa nao? Kodi ndikhoza kuyera ndi miyeso yoipa, ndi thumba la miyala yonyenga? Pakuti anthu ake olemera adzala ndi chiwawa, ndi okhalamo amanena bodza, ndi lilime lao limachita monyenga m'kamwa mwao. Chifukwa chake Inenso ndakukantha ndi kukupweteketsa; ndakupulula chifukwa cha zochimwa zako. Udzadya koma osakhuta; ndi njala yako idzakhala pakati pako; ndipo udzachotsa koma osalanditsa; ndi ichi wachilanditsa ndidzachipereka kulupanga. Udzafesa koma osacheka; udzaponda azitona koma osadzola mafuta; udzaponda mphesa koma osamwa vinyo. Pakuti asunga malemba a Omuri, ndi ntchito za nyumba ya Ahabu, ndipo mumayenda m'uphungu wao; kuti ndikusandulize bwinja, ndi okhalamo chotsonya; ndipo mudzasenza chitonzo cha anthu anga. Kalanga ine! Pakuti ndikunga atapulula zipatso za m'mwamvu, atakunkha m'munda wamphesa; palibe mphesa zakudya; moyo wanga ukhumba nkhuyu yoyamba kupsa. Watha wachifundo m'dziko, palibe woongoka mwa anthu; onsewo alalira mwazi; yense asaka mbale wake ndi ukonde. Manja ao onse awiri agwira choipa kuchichita ndi changu; kalonga apempha, ndi woweruza aweruza chifukwa cha mphotho; ndi wamkuluyo angonena chosakaza moyo wake; ndipo achiluka pamodzi. Wokoma wa iwo akunga mitungwi; woongoka wao aipa koposa mpanda waminga; tsiku la alonda ako la kulangidwa kwako lafika, tsopano kwafika kuthedwa nzeru kwao. Musakhulupirira bwenzi, musatama bwenzi loyanja; usamtsegulire pakhomo pakamwa pako, ngakhale kwa iye wogona m'fukato mwako. Pakuti mwana wamwamuna apeputsa atate, mwana wamkazi aukira amake, mpongozi aukira mpongozi wake; adani ake a munthu ndiwo a m'nyumba yake. Koma ine, ndidzadikira Yehova; ndidzalindirira Mulungu wa chipulumutso changa; Mulungu wanga adzandimvera. Usandiseka, mdani wangawe; pakugwa ine ndidzaukanso; pokhala ine mumdima Yehova adzakhala kuunika kwanga. Ndidzasenza mkwiyo wa Yehova, chifukwa ndamchimwira, mpaka andinenera mlandu wanga, ndi kundiweruzira mlandu wanga; adzanditulutsira kwa kuunika, ndipo ndidzapenya chilungamo chake. Pamenepo mdani wanga adzachiona, ndi manyazi adzamkuta iye amene adati kwa ine, Ali kuti Yehova Mulungu wako? Maso anga adzamuona; tsopano adzampondereza ngati thope la m'miseu. Tsiku lakumanga malinga ako, tsiku lomwelo lembalo lidzachotsedwa kunka kutali. Tsiku lomwelo adzadza kwa iwe, kuchokera ku Asiriya ndi midzi ya ku Ejipito, kuyambira ku Ejipito kufikira ku Mtsinje, ndi kuyambira kunyanja kufikira kunyanja, ndi kuyambira kuphiri kufikira kuphiri. Koma dziko lidzakhala labwinja chifukwa cha iwo okhalamo, mwa zipatso za machitidwe ao. Mudyetse anthu anu ndi ndodo yanu, nkhosa za cholowa chanu zokhala pa zokha m'nkhalango pakati pa Karimele, zidye m'Basani ndi m'Giliyadi masiku a kale lomwe. Monga masiku a kutuluka kwako m'dziko la Ejipito ndidzamuonetsa zodabwitsa. Amitundu adzaona nadzachita manyazi ndi mphamvu yao yonse; adzagwira pakamwa, m'makutu mwao mudzagontha. Adzanyambita fumbi ngati njoka; ngati zokwawa za padziko, adzanjenjemera potuluka m'ngaka mwao; adzafika kwa Yehova Mulungu wao ndi mantha, nadzaopa chifukwa cha iwe. Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakukhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a cholowa chake? Sasunga mkwiyo wake kunthawi yonse popeza akondwera nacho chifundo. Adzabwera, nadzatichitira nsoni; adzagonjetsa mphulupulu zathu; ndipo mudzataya zochimwa zao zonse m'nyanja yakuya. Mudzapatsa kwa Yakobo choonadi, ndi kwa Abrahamu chifundo chimene munalumbirira makolo athu kuyambira masiku a kale lomwe. Katundu wa Ninive. Buku la masomphenya a Nahumu wa ku Elikosi. Yehova ndiye Mulungu wansanje, nabwezera chilango; Yehova ndiye wobwezera chilango, ndi waukali ndithu; Yehova ndiye wobwezera chilango oyambana naye, nasungira mkwiyo pa adani ake. Yehova ndiye wolekerera mkwiyo, koma wa mphamvu yaikulu; ndi wosamasula ndithu wopalamula; njira ya Yehova ili m'kamvulumvulu ndi mumkuntho; ndipo mitambo ndiyo fumbi la mapazi ake. Adzudzula nyanja, naiphwetsa, naumitsa mitsinje yonse; Basani ndi Karimele afota, ndi duwa la ku Lebanoni linyala. Mapiri agwedezeka chifukwa cha Iye, ndi zitunda zisungunuka; ndi dziko lapansi likwezeka pamaso pake, ndi maiko ndi onse okhala m'mwemo. Adzaima ndani pa kulunda kwake? Ndipo adzakhalitsa ndani pa mkwiyo wake wotentha? Ukali wake utsanulidwa ngati moto, ndi matanthwe asweka ndi Iye. Yehova ali wabwino, ndiye polimbikirapo tsiku la msauko; ndipo adziwa iwo omkhulupirira Iye. Koma ndi chigumula chosefukira adzatha konse malo ake, nadzapirikitsira adani ake kumdima. Mulingaliranji chotsutsana ndi Yehova? Iye adzatha psiti; nsautso siidzauka kawiri. Pakuti chinkana akunga minga yoyangayanga, naledzera nacho choledzeretsa chao, adzathedwa konse ngati chiputu chouma. Mwa iwe watuluka wina wolingalira choipa chotsutsana ndi Yehova, ndiye phungu wopanda pake. Atero Yehova: Angakhale iwo ali ndi mphamvu yokwanira, nachuluka momwemo, koma momwemonso adzasalikidwa, ndipo iye adzapitiratu. Chinkana ndakuzunza iwe, sindidzakuzunzanso. Koma tsopano ndidzathyola ndi kukuchotsera goli lake, ndipo ndidzadula zomangira zako. Ndipo Yehova walamulira za iwe kuti asabzalidwenso ena a dzina lako; m'nyumba ya milungu yako ndidzachotsa fano losema ndi fano loyenga; ndidzakukonzerapo manda, pakuti iwe ndiwe wopepuka. Taonani pamapiri mapazi a iye wakulalikira uthenga wabwino, wakubukitsa mtendere! Chita chikondwerero chako, Yuda, kwaniritsa zowinda zako; pakuti wopanda pakeyo sadzapitanso mwa iwe; iye waonongeka konse. Wophwanyayo wakwera pamaso pako; sunga linga, yang'anira panjira, limbitsa m'chuuno mwako, limbikitsatu mphamvu yako. Pakuti Yehova abwezeranso ukulu wake wa Yakobo ngati ukulu wake wa Israele; pakuti okhuthula anawakhuthula, naipsa nthambi zake za mpesa. Zikopa za amphamvu ake zasanduka zofiira, ngwazi zivala mlangali; magaleta anyezimira ndi chitsulo tsiku la kukonzera kwake, ndi mikondo itinthidwa. Magaleta achita mkokomo m'miseu, akankhana m'makwalala; maonekedwe ao akunga miuni, athamanga ngati mphezi. Akumbukira omveka ake; akhumudwa m'kupita kwao, afulumira kulinga lake, ndi chotchinjiriza chakonzeka. Pa zipata za mitsinje patseguka, ndi chinyumba chasungunuka. Chatsimikizika, avulidwa, atengedwa, adzakazi ake alira ngati mau a nkhunda, nadziguguda pachifuwa pao. Koma Ninive wakhala chiyambire chake ngati thamanda lamadzi; koma athawa. Imani, Imani! Ati, koma palibe wocheuka. Funkhani siliva, funkhani golide; pakuti palibe kutha kwake kwa zosungikazo, kwa chuma cha zipangizo zofunika zilizonse. Ndiye mopanda kanthu mwakemo ndi mwachabe, ndi wopasuka; ndi mtima usungunuka, ndi maondo aombana, ndi m'zuuno zonse muwawa, ndi nkhope zao zatumbuluka. Ili kuti ngaka ya mikango, ndi podyera misona ya mikango, kumene mkango, waumuna ndi waukazi, ukayenda ndi mwana wa mkango, kopanda wakuiposa? Mkangowo unamwetula zofikira ana ake, nusamira yaikazi yake, nudzaza mapanga ake ndi nyama, ngaka zake ndi zojiwa. Taona, nditsutsana nawe, ati Yehova wa makamu, ndipo ndidzatentha magaleta ake m'utsi; ndi lupanga lidzadya misona yako ya mkango; ndipo ndidzachotsa zofunkha zako pa dziko lapansi, ndi mau a mithenga yako sadzamvekanso. Tsoka mudzi wa mwazi! Udzala nao mabodza ndi zachifwamba; zachifwamba sizidukiza. Kumveka kwa chikoti, ndi mkokomo wa kuyenda kwa njinga za magaleta; ndi kaphatakaphata wa akavalo, ndi gwegwegwe wa magaleta; munthu wokwera pa kavalo, ndi lupanga lonyezimira, ndi mkondo wong'anipa; ndi aunyinji ophedwa, ndi chimulu cha mitembo, palibe kutha zitanda; angokhumudwa ndi zitanda; chifukwa cha chiwerewere chochuluka cha wachiwerewere wokongola, ndiye mkaziyo mwini nyanga, wakugulitsa amitundu mwa chiwerewere chake, ndi mabanja mwa nyanga zake. Taona, nditsutsana nawe, ati Yehova wa makamu, ndidzaphimba nkhope yako ndi nsalu yako yoyesa mthendene; ndipo ndidzaonetsa amitundu umaliseche wako, ndi mafumu manyazi ako. Ndipo ndidzakuponyera zonyansa, ndi kukuchititsa manyazi, ndi kukuika chopenyapo. Ndipo kudzali kuti onse akupenyerera iwe adzakuthawa, nadzati, Ninive wapasuka, adzamlira maliro ndani? Ndidzakufunira kuti akukutonthoza? Kodi uli wabwino woposa No-Amoni, wokhala pakati pa mitsinje wozingidwa ndi madzi; amene tchemba lake ndilo nyanja, ndi linga lake ndilo nyanja? Kusi ndi Ejipito ndiwo mphamvu yake, ndiyo yosatha, Puti ndi Libiya ndiwo akukuthandiza. Koma iye anatengedwa, analowa ndende; ana ake a makanda anaphwanyika polekeza pake pa miseu yake yonse; ndi pa omveka ake anachita maere, ndi akulu ake onse anamangidwa maunyolo. Iwenso udzaledzera, udzabisala; iwenso udzafunanso polimbikira chifukwa cha mdani. Malinga ako onse adzanga mikuyu ndi nkhuyu zoyamba kupsa; akagwedeza zingokugwa m'kamwa mwa wakudya. Taona, anthu ako m'kati mwako akunga akazi, zipata za dziko lako zatsegulidwira adani ako papakulu; moto watha mipingiridzo yako. Udzitungiretu madzi a nthawi yokumangira misasa, limbikitsa malinga ako, lowa kuthope, ponda dothi, limbitsa ng'anjo yanjerwa. Pomwepo moto udzatha iwe; lupanga lidzakuononga; lidzatha iwe ngati chirimamine; udzichulukitse ngati chirimamine, udzichulukitse ngati dzombe. Wachulukitsa amalonda ako koposa nyenyezi za kuthambo; chirimamine anyambita, nauluka, nathawa. Ovala korona ako akunga dzombe, ndi akazembe, ndi akazemba ako ngati ziwalamsatsi zakutera m'matchinga tsiku lachisanu, koma likafundukula dzuwa ziuluka nizithawa, ndi kumene zinakhalako sikudziwikanso. Abusa ako aodzera, mfumu ya ku Asiriya; omveka ako apumula; anthu ako amwazika pamapiri, ndipo palibe wakuwasonkhanitsa. Palibe chakulunzitsa kuthyoka kwako; bala lako liwawa; onse akumva mbiri yako akuombera manja; pakuti ndaniyo kuipa kwako sikunampitapitabe? Katundu adamuona mneneri Habakuku Yehova, ndidzafuula mpaka liti osamva Inu? Ndifuulira kwa Inu za chiwawa, koma simupulumutsa. Mundionetseranji zopanda pake, ndi kundionetsa zovuta? Pakuti kufunkha ndi chiwawa zili pamaso panga; ndipo pali ndeu, nauka makani. Pakuti chilamulo chalekeka, ndi chiweruzo sichitulukira konse; popeza woipa azinga wolungama, chifukwa chake chiweruzo chituluka chopindika. Penyani mwa amitundu, penyetsetsani, nimudabwe kwakukulu, pakuti ndichita ntchito masiku anu, imene simudzavomera chinkana akufotokozerani. Pakuti taonani, ndiukitsa Ababiloni, mtundu uja wowawa ndi waliwiro, wopitira pa chitando cha dziko lapansi, kulowa m'malo mosati mwao, mukhale mwaomwao. Ali oopsa, achititsa mantha, chiweruzo chao ndi ukulu wao zituluka kwa iwo eni. Akavalo ao aposa anyalugwe liwiro lao, aposa mimbulu ya madzulo ukali wao, ndipo apakavalo ao atanda; inde apakavalo ao afumira kutali; auluka ngati chiombankhanga chofulumira kudya. Adzera chiwawa onsewo; nkhope zao zikhazikika zolunjika m'tsogolo; asonkhanitsa andende ngati mchenga. Inde anyoza mafumu, aseka akalonga; aseka linga lililonse; popeza aunjika dothi, nalilanda. Pamenepo adzapitirira ngati mphepo, nadzalakwa ndi kupalamula, iye amene aiyesa mphamvu yake mulungu wake. Si ndinu wachikhalire, Yehova Mulungu wanga, wopatulika wanga? Sitidzafa. Yehova munamuikiratu kuti aweruzidwe; ndipo Inu, Thanthwe, munamkhazika kuti alangidwe. Inu wa maso osalakwa, osapenya choipa, osakhoza kupenyerera chovuta, mupenyereranji iwo akuchita mochenjerera, ndi kukhala chete pamene woipa ammeza munthu wolungama woposa iye mwini; ndi kuyesa anthu ngati nsomba za m'nyanja, ngati zokwawa zopanda wakuzilamulira. Aziwedza zonse ndi mbedza, azigwira m'ukonde wake, nazisonkhanitsa m'khoka mwake; chifukwa chake asekera nakondwerera. Chifukwa chake aphera nsembe ukonde wake, nafukizira khoka lake, pakuti mwa izi gawo lake lilemera, ndi chakudya chake chichuluka. Kodi m'mwemo adzakhuthula m'ukonde mwake osaleka kuphabe amitundu? Ndidzaima pa dindiro langa ndi kudziika palinga, ndipo ndidzayang'anira ndione ngati adzanenanji mwa ine, ngatinso ndidzamyankha chiyani pa choneneza changa. Ndipo Yehova anandiyankha nati, Lembera masomphenyawo, nuwachenutse pamagome, kuti awawerenge mofulumira. Pakuti masomphenyawo alindira nyengo yoikidwiratu, ndipo afulumirira potsirizira pake, osanama; akachedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza. Taonani, moyo wake udzikuza, wosaongoka m'kati mwake; koma wolungama adzakhala ndi moyo mwa chikhulupiriro chake. Ndiponso vinyo ngwonyenga, ngati munthu wodzikuza, wosakhala kwao; wakukulitsa chikhumbo chake ngati kunsi kwa manda, akunga imfa, yosakhuta, koma adzisonkhanitsira amitundu onse, nadzimemezera mitundu yonse ya anthu. Kodi sadzamnenera fanizo onsewo, ndi mwambi womnyodola, ndi kuti, Tsoka iye wochulukitsa zimene sizili zake? Mpaka liti? Iye wodzisenzera zigwiriro. Sadzauka kodi modzidzimuka iwo amene adzakuluma, ndi kugalamuka iwo amene adzakugwedezetsa; ndipo udzakhala zofunkha zao? Popeza iwe wafunkha amitundu ambiri, otsala onse a mitundu ya anthu adzakufunkha iwe; chifukwa cha mwazi wa anthu, ndi chiwawa chochitikira dziko, mudzi, ndi onse okhalamo. Tsoka iye wakupindulitsira nyumba yake phindu loipa, kuti aike chisanja chake ponyamuka, kuti alanditsidwe m'dzanja la choipa! Wapangira nyumba yako chamanyazi, pakuononga mitundu yambiri ya anthu, ndipo wachimwira moyo wako. Pakuti mwala wa m'khoma ufuula, ndi mtanda wa kuphaso udzauvomereza. Tsoka iye wakumanga mudzi ndi mwazi, nakhazikitsa mudzi ndi chisalungamo! Taonani, sichichokera kwa Yehova wa makamu kodi kuti mitundu ya anthu ingogwirira moto ntchito, ndi anthu angodzilemetsa pa zopanda pake? Pakuti dziko lapansi lidzadzazidwa ndi chidziwitso cha ulemerero wa Yehova, monga madzi amphimba pansi pa nyanja. Tsoka wakuninkha mnzake chakumwa, ndi kuonjezako mankhwala ako, ndi kumledzeretsa, kuti upenyerere manyazi ao! Udzazidwa nao manyazi m'malo mwa ulemerero; imwa iwenso, nukhale wosadulidwa; chikho cha dzanja lamanja la Yehova chidzatembenukira iwe, ndi kusanza kwa manyazi kudzakhala pa ulemerero wako. Pakuti chiwawa chidachitikira Lebanoni chidzakukuta, ndi chionongeko cha nyama chidzakuopsa; chifukwa cha mwazi wa anthu, ndi chiwawa chochitidwira dziko, mudzi, ndi onse okhalamo. Apindulanji nalo fano losema, kuti wakulipanga analisema; fano loyenga ndi mphunzitsi wamabodza, kuti wakulipanga alikhulupirira, atapanga mafano osanena mau? Tsoka iye wakunena kwa mtengo, Galamuka; ndi kwa mwala wosalankhula, Nyamuka! Kodi ichi chiphunzitsa? Taona chakutidwa ndi golide ndi siliva, ndi m'kati mwake mulibe mpweya konse. Koma Yehova ali m'Kachisi wake wopatulika; dziko lonse lapansi likhale chete pamaso pake. Pemphero la Habakuku mneneri, pa Sigionoti. Yehova, ndinamva mbiri yanu ndi mantha; Yehova, tsitsimutsani ntchito yanu pakati pa zaka, pakati pa zaka mudziwitse; pa mkwiyo mukumbukire chifundo. Mulungu anafuma ku Temani, ndi Woyerayo kuphiri la Parani. Ulemerero wake unaphimba miyamba, ndi dziko lapansi linadzala ndi kumlemekeza. Ndi kunyezimira kwake kunanga kuunika; anali nayo mitsitsi ya dzuwa yotuluka m'dzanja lake, ndi komweko kunabisika mphamvu yake. Patsogolo pake panapita mliri, ndi makala amoto anatuluka pa mapazi ake. Anaimirira, nandengulitsa dziko lapansi; anapenya, nanjenjemeretsa amitundu; ndi mapiri achikhalire anamwazika, zitunda za kale lomwe zinawerama; mayendedwe ake ndiwo a kale lomwe. Ndinaona mahema a Kusani ali mkusauka; nsalu zotchinga za dziko la Midiyani zinanjenjemera. Kodi Yehova anaipidwa nayo mitsinje? Mkwiyo wanu unali pamitsinje kodi, kapena ukali wanu panyanja, kuti munayenda pa akavalo anu, pa magaleta anu a chipulumutso? Munapombosola uta wanu; malumbiro analumbirira mafuko anali mau oona. Munang'amba dziko lapansi ndi mitsinje. Mapiri anakuonani, namva zowawa; chigumula cha madzi chinapita; madzi akuya anamveketsa mau ake, nakweza manja ake m'mwamba. Dzuwa ndi mwezi zinaima njera mokhala mwao; pa kuunika kwa mivi yanu popita iyo. Pa kung'anipa kwa nthungo yanu yonyezimira. Munaponda dziko ndi kulunda, munapuntha amitundu ndi mkwiyo. Munatulukira chipulumutso cha anthu anu, chipulumutso cha odzozedwa anu; munakantha mutu wa nyumba ya woipa, ndi kufukula maziko kufikira m'khosi. Munapyoza ndi maluti ake mutu wa ankhondo ake; anadza ngati kamvulumvulu kundimwaza; kukondwerera kwao kunanga kufuna kutha ozunzika mobisika. Munaponda panyanja ndi akavalo anu, madzi amphamvu anaunjikana mulu. Ndinamva, ndi m'mimba mwanga munabwadamuka, milomo yanga inanthunthumira pamau, m'mafupa mwanga mudalowa chivundi, ndipo ndinanjenjemera m'malo mwanga; kuti ndipumule tsiku lamsauko, pamene akwerera anthu kuti ayambane nao ndi makamu. Chinkana mkuyu suphuka, kungakhale kulibe zipatso kumpesa; yalephera ntchito ya azitona, ndi m'minda m'mosapatsa chakudya; ndi zoweta zachotsedwa kukhola, palibenso ng'ombe m'makola mwao; koma ndidzakondwera mwa Yehova, ndidzasekerera mwa Mulungu wa chipulumutso changa. Yehova, Ambuye, ndiye mphamvu yanga, asanduliza mapazi anga ngati a mbawala, nadzandipondetsa pa misanje yanga. Mau a Yehova amene anadza kwa Zefaniya mwana wa Kusi, mwana wa Gedaliya, mwana wa Amariya, mwana wa Hezekiya, masiku a Yosiya, mwana wa Amoni mfumu ya Yuda. Kuzitha ndidzazitha zonse kuzichotsa panthaka, ati Yehova. Ndidzatha munthu ndi nyama; ndidzatha mbalame za m'mlengalenga, ndi nsomba za m'nyanja, ndi zokhumudwitsa pamodzi ndi oipa; ndipo ndidzaononga anthu kuwachotsa panthaka, ati Yehova. Ndipo ndidzatambasulira dzanja langa pa Yuda, ndi pa onse okhala m'Yerusalemu; ndipo ndidzaononga otsala a Baala kuwachotsa m'malo muno, ndi dzina la Akemari pamodzi ndi ansembe; ndi iwo akulambira khamu la kumwamba pamwamba pa matsindwi; ndi iwo akulambira, akulumbira pali Yehova, nalumbiranso pali mfumu; ndi iwo akubwerera osamtsata Yehova; ndi osamfuna Yehova, kapena kufunsira kwa Iye. Khala chete pamaso pa Ambuye Yehova; pakuti tsiku la Yehova liyandikira; pakuti Yehova wakonzeratu nsembe, anapatula oitanidwa ake. Ndipo kudzachitika tsiku la nsembe ya Yehova, kuti ndidzalanga akalonga ndi ana a mfumu, ndi onse akuvala chovala chachilendo. Ndipo tsiku ilo ndidzalanga olumpha chiundo, nadzaza nyumba ya mbuye wao ndi chiwawa ndi chinyengo. Ndipo tsiku ilo, ati Yehova, kudzakhala phokoso lakulira lochokera kuchipata chansomba, ndi kuchema kochokera kudera lachiwiri, ndi kugamuka kwakukulu kochokera kuzitunda. Chemani okhala m'chigwa, pakuti amalonda onse atayika, onsewo osenza siliva aonongeka. Ndipo kudzachitika nthawi yomweyi kuti ndidzasanthula Yerusalemu ndi nyali, ndipo ndidzalanga amunawo okhala ndi nsenga, onena m'mtima mwao, Yehova sachita chokoma, kapena kuchita choipa. Ndipo zolemera zao zidzakhala zakufunkhidwa; ndi nyumba zao zabwinja; adzamangadi nyumba, koma sadzagonamo; adzaoka minda yampesa koma sadzamwa vinyo wake. Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi, lili pafupi lifulumira kudza, mau a tsiku la Yehova; munthu wamphamvu adzalirapo mowawa mtima. Tsikulo ndi tsiku la mkwiyo, tsiku la msauko ndi lopsinja tsiku la bwinja, ndi chipasuko, tsiku la mdima ndi la chisisira, tsiku la mitambo ndi lakuda bii; tsiku la lipenga ndi lakufuulira midzi yamlinga, ndi nsanja zazitali za kungodya. Ndipo ndidzatengera anthu zowapsinja, kuti adzayenda ngati anthu akhungu, popeza anachimwira Yehova; ndi mwazi wao udzatsanulidwa ngati fumbi, ndi nyama yao idzanga ndowe. Ngakhale siliva wao, ngakhale golide wao sizidzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova; koma dziko lonse lidzatha ndi moto wa nsanje yake; pakuti adzachita chakutsiriza, mofulumira, onse okhala m'dziko. Dzisanthuleni, inde santhulani; inu mtundu wosakhumba kanthu; lamulo lisanabale, tsiku lisanapitirire ngati mungu, usanakugwereni mkwiyo waukali wa Yehova, lisanakugwereni tsiku la mkwiyo wa Yehova. Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m'dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova. Pakuti Gaza adzasiyidwa, ndi Asikeloni adzakhala bwinja; adzaingitsa Asidodi usana, ndi Ekeroni adzazulidwa. Tsoka, okhala m'dziko la kunyanja, mtundu wa Akereti! Mau a Yehova atsutsana nawe, Kanani, dziko la Afilisti; ndidzakuononga, kuti pasakhale wokhala m'dziko. Ndipo dziko la kunyanja lidzakhala busa, ndi mapanga a abusa, ndi makola a zoweta. Ndipo dziko la kunyanja lidzakhala la otsala a nyumba ya Yuda; adzadyetsa zoweta zao pamenepo; madzulo adzagona m'nyumba za Asikeloni; pakuti Yehova Mulungu wao adzawazonda, nadzabweza undende wao. Ndinamva kutonza kwa Mowabu ndi matukwano a ana a Amoni, zimene anatonza nazo anthu anga, ndi kudzikuza pa malire ao. Chifukwa chake, pali moyo wanga, ati Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Zedi Mowabu adzakhala ngati Sodomu, ndi ana a Amoni ngati Gomora, pochuluka khwisa ndi maenje a mchere, ndi bwinja losatha; otsala a anthu anga adzalanda zao, ndi otsala a mtundu wa anthu anga adzawalandira akhale cholowa chao. Ichi adzakhala nacho m'malo mwa kudzikuza kwao, chifukwa anatonza, nadzikuza pa anthu a Yehova wa makamu. Yehova adzawakhalira woopsa; pakuti adzaondetsa milungu yonse ya pa dziko lapansi; ndipo adzamlambira Iye, yense pamalo pake, a m'zisumbu zonse za amitundu. Inunso Akusi, mudzaphedwa ndi lupanga langa. Ndipo adzatambasulira dzanja lake kumpoto nadzaononga Asiriya, nadzasanduliza Ninive akhale bwinja, wouma ngati chipululu. Ndipo zoweta zidzagona pansi pakati pake; nyama zonse za mitundumitundu; ndi vuwo ndi nungu zidzakhala m'mitu ya nsanamira zake; adzaimba mau ao m'mazenera; paziundo padzakhala chipasuko; pakuti anagadamula ntchito yake ya mkungudza. Uwu ndi mudzi wosekererawo unakhala wosasamalira, unanena m'mtima mwake, Ine ndine, ndi wopanda ine palibe wina; ha! Wasanduka bwinja, mogonera nyama za kuthengo! Yense wakuupitirira adzatsonya mtsonyo, ndi kupukusa mutu. Tsoka uyo wopanduka, ndi wodetsedwa, ndiye mudzi wozunza! Sanamvera mau, sanalole kulangizidwa; sanakhulupirire Yehova, sanayandikire kwa Mulungu wake. Akalonga ake m'kati mwake ndiwo mikango yobangula; oweruza ake ndi mimbulu ya madzulo, sasiya kanthu ka mawa. Aneneri ake ndiwo anthu a matukutuku ndi onyenga; ansembe ao anaipsa malo opatulika, napotoza chilamulo. Yehova pakati pake ali wolungama; sadzachita chosalungama, m'mawa ndi m'mawa aonetsera chiweruzo chake poyera, chosasowa kanthu; koma wosalungama sadziwa manyazi. Ndaononga amitundu; nsanja zao za kungodya nza bwinja, ndapasula miseu yao, palibe wopitapo; midzi yao yaonongeka, palibe munthu, palibe wokhalamo. Ndinati, Zedi udzandiopa Ine, udzalola kulangizidwa, kuti pokhala pake pasaonongeke, monga mwa zonse ndamuikira; koma analawirira mamawa, navunditsa machitidwe ao onse. Chifukwa chake, mundilindire, ati Yehova, kufikira tsiku loukira Ine zofunkha; pakuti ndatsimikiza mtima Ine kusonkhanitsa amitundu, kuti ndimemeze maufumu kuwatsanulira kulunda kwanga, ndilo mkwiyo wanga wonse waukali; pakuti dziko lonse lapansi lidzathedwa ndi moto wa nsanje yanga. Pakuti pamenepo ndidzapatsa mitundu ya anthu mlomo woyera, kuti onsewa aitanire pa dzina la Yehova kumtumikira ndi mtima umodzi. Kuchokera tsidya lija la mitsinje ya Kusi ondipembedza, ndiwo mwana wamkazi wa obalalika anga, adzabwera nacho chopereka changa. Tsiku ilo sudzachita manyazi ndi zochita zako zonse unandilakwira nazo; pakuti pamenepo ndidzachotsa pakati pako amene akondwera ndi kudzikuza kwako, ndipo sudzachita kudzikuzanso m'phiri langa lopatulika. Koma ndidzasiya pakati pako anthu ozunzika ndi osauka, ndipo iwo adzakhulupirira dzina la Yehova. Otsala a Israele sadzachita chosalungama, kapena kunena mabodza; ndi m'kamwa mwao simudzapezeka lilime lonyenga; pakuti adzadya nadzagona pansi, ndi palibe wakuwaopsa. Imba, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula, Israele; kondwera nusekerere ndi mtima wonse, mwana wamkazi wa Yerusalemu. Yehova wachotsa maweruzo ako, anataya kunja mdani wako; mfumu ya Israele, Yehova, ali pakati pako, sudzaopanso choipa. Tsiku lomwelo adzati kwa Yerusalemu, Usaopa Ziyoni, manja anu asakhale olefuka. Yehova Mulungu wako ali pakati pako, wamphamvu wakupulumutsa; adzakondwera nawe ndi chimwemwe, adzakhala wopanda thamo m'chikondi chake; adzasekerera nawe ndi kuimbirapo. Ndidzasonkhanitsa iwo akulirira msonkhano woikika, ndiwo a mwa iwe, amene katundu wake anawakhalira mtonzo. Taonani, nthawi yomweyo ndidzachita nao onse akuzunza iwe; ndipo ndidzapulumutsa wotsimphinayo, ndi kusonkhanitsa wopirikitsidwayo; ndipo ndidzawaika akhale chilemekezo ndi dzina, iwo amene manyazi ao anali m'dziko lonse. Nthawi yomweyo ndidzakulowetsani, ndi nthawi yomweyo ndidzakusonkhanitsani; pakuti ndidzakuikani mukhale dzina, ndi chilemekezo mwa mitundu yonse ya anthu a pa dziko lapansi, pamene ndibweza undende wanu pamaso panu, ati Yehova. Chaka chachiwiri cha mfumu Dariusi, mwezi wachisanu ndi chimodzi, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri kwa Zerubabele mwana wa Sealatiele, chiwanga cha Yuda, ndi kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu, akuti, Anthu awa anena, Nthawi siinafike, nthawi yakumanga nyumba ya Yehova. Pamenepo mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri, ndi kuti, Kodi imeneyi ndiyo nthawi yakuti inu nokha mukhala m'nyumba zanu zochingidwa m'katimo, ndi nyumba iyi ikhale yopasuka? Chifukwa chake tsono, atero Yehova wa makamu: Mtima wanu usamalire njira zanu. Mwabzala zambiri, koma mututa pang'ono; mukudya, koma osakhuta; mukumwa, koma osakoledwa; mudziveka, koma palibe wofundidwa; ndi iye wolembedwa ntchito yakulipidwa alandirira kulipirako m'thumba lobooka. Atero Yehova wa makamu: Mtima wanu usamalire njira zanu. Kwerani kudziko la mapiri, ndi kukwera nayo mitengo, nimumange nyumbayi; ndipo kudzandikomera, ndipo ndidzalemekezedwa, ati Yehova. Munayembekezera zambiri, koma taonani, pang'ono; ndipo, mutabwera napo kwanu, ndinauzirapo. Chifukwa ninji? Ati Yehova wa makamu. Chifukwa cha nyumba yanga yokhala yopasuka, ndipo nuthamangira yense kunyumba kwake. M'mwemo chifukwa cha inu kumwamba kukaniza mame, ndi nthaka ikaniza zipatso zake. Ndipo ndinaitana chilala chidzere dziko, ndi mapiri, ndi tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi zimene ibala nthaka, ndi anthu, ndi zoweta, ndi ntchito zonse za manja. Pamenepo Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi otsala onse a anthu, anamvera mau a Yehova Mulungu wao, ndi mau a Hagai mneneri, monga Yehova Mulungu wao adamtuma; ndipo anthu anaopa pamaso pa Yehova. Ndipo Hagai mthenga wa Yehova, m'uthenga wa Yehova ananena ndi anthu, ndi kuti, Ine ndili nanu, ati Yehova. Ndipo Yehova anautsa mzimu wa Zerubabele mwana wa Sealatiele, chiwanga cha Yuda, ndi mzimu wa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi mzimu wa otsala onse a anthu, ndipo anadza nagwira ntchito m'nyumba ya Yehova wa makamu, Mulungu wao, tsiku la makumi awiri ndi anai la mwezi, mwezi wachisanu ndi chimodzi, chaka chachiwiri cha mfumu Dariusi. Mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku la makumi awiri ndi chimodzi la mweziwo, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri, ndi kuti, Unenetu kwa Zerubabele, mwana wa Sealatiele, chiwanga cha Yuda, ndi kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi kwa otsala a anthu, kuti, Adatsala ndani mwa inu amene anaona nyumba iyi m'ulemerero wake woyamba? Ndipo muiona yotani tsopano? Kodi siikhala m'maso mwanu ngati chabe? Koma limbika tsopano, Zerubabele, ati Yehova; ulimbikenso Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe; ndipo mulimbike inu nonse anthu a m'dziko, ati Yehova, ndi kuchita; pakuti Ine ndili pamodzi ndi inu, ati Yehova wa makamu; monga momwe ndinapangana nanu muja munatuluka m'Ejipito, ndi Mzimu wanga unakhala pakati pa inu; musamaopa inu. Pakuti atero Yehova wa makamu: Kamodzinso, katsala kanthawi, ndidzagwedeza miyamba ndi dziko lapansi, ndi nyanja, ndi mtunda womwe; ndipo ndidzagwedeza amitundu onse, ndi zofunika za amitundu onse zidzafika, ndipo ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero, ati Yehova wa makamu. Siliva ndi wanga, ya golide ndi wanga, ati Yehova wa makamu. Ulemerero wotsiriza wa nyumba iyi udzaposa woyambawo, ati Yehova wa makamu; ndipo m'malo muno ndidzapatsa mtendere, ati Yehova wa makamu. Tsiku la makumi awiri ndi anai la mwezi wachisanu ndi chinai, chaka chachiwiri cha Dariusi, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu: Funsatu ansembe za chilamulo, ndi kuti, Munthu akanyamulira nyama yopatulika m'ngudulira, nakhudza mkate, kapena ndiwo, kapena vinyo, kapena mafuta, kapena chakudya chilichonse, ndi ngudulira, kodi chisandulika chopatulika? Ndipo ansembe anayankha nati, Iai. Pamenepo Hagai anati, Munthu wodetsedwa ndi mtembo akakhudza kanthu ka izi, kodi kali kodetsedwa kanthuka? Ndipo ansembe anayankha nati, Kadzakhala kodetsedwa. Ndipo Hagai anayankha, nati, Momwemo anthu awa, ndi momwemo mtundu uwu pamaso panga, ati Yehova; ndi momwemo ntchito iliyonse ya manja ao; ndi ichi achipereka, chili chodetsedwa. Ndipo tsono, samalirani, kuyambira lero ndi m'tsogolomo, kuti, kusanaikidwe mwala pa mwala m'Kachisi wa Yehova, pamenepo ponse munthu akadza ku mulu woyenera miyeso makumi awiri, pali khumi yokha; munthu akadza ku choponderamo mphesa kudzatunga mbiya makumi asanu, pali makumi awiri okha. Ndinakukanthani ndi chinsikwi ndi chinoni ndi matalala m'ntchito zonse za manja anu, koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova. Musamalire, kuyambira lero ndi m'tsogolo, kuyambira tsiku la makumi awiri ndi chinai la mwezi wachisanu ndi chinai, kuyambira tsiku lija anamanga maziko a Kachisi wa Yehova, samalirani. Kodi mbeu ikali m'nkhokwe? Ngakhale mpesa, ndi mkuyu, ndi khangaza ndi azitona sizinabala; kuyambira lero lino ndidzakudalitsani. Ndipo mau a Yehova anadza nthawi yachiwiri kwa Hagai tsiku la makumi awiri la mwezi, ndi kuti, Nena ndi Zerubabele chiwanga cha Yuda, kuti, Ndidzagwedeza miyamba ndi dziko lapansi; ndipo ndidzagubuduza mipando yachifumu ya maufumu, ndidzaononga mphamvu ya maufumu a amitundu; ndidzagubuduza magaleta ndi iwo akuyendapo; ndi akavalo ndi apakavalo adzatsika, yense ndi lupanga la mbale wake. Tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, ndidzakutenga, Zerubabele mtumiki wanga, mwana wa Sealatiele, ati Yehova, ndi kuika iwe ngati mphete yosindikizira; pakuti ndakusankha, ati Yehova wa makamu. Mwezi wachisanu ndi chitatu, chaka chachiwiri cha Dariusi, mau a Yehova anadza kwa Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido mneneri, ndi kuti, Yehova anakwiya kwambiri ndi makolo anu. Chifukwa chake uziti nao, Atero Yehova wa makamu: Bwererani kudza kwa Ine, ati Yehova wa makamu, ndipo Ine ndidzabwerera kudza kwa inu, ati Yehova wa makamu. Musamakhala ngati makolo anu, amene aneneri akale anawafuulira, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu Bwereranitu kuleka njira zanu zoipa, ndi machitidwe anu oipa; koma sanamve, kapena kumvera Ine ati Yehova. Makolo anu, ali kuti iwowo? Ndi aneneri, akhala ndi moyo kosatha kodi? Koma mau anga ndi malemba anga, amene ndinalamulira atumiki anga aneneriwo, kodi sanawapeze makolo anu? Ndipo anabwera, nati, Monga umo Yehova wa makamu analingirira kutichitira ife, monga mwa njira zathu ndi monga mwa machitidwe athu, momwemo anatichitira. Tsiku la makumi awiri ndi chinai la mwezi wakhumi ndi chimodzi, ndiwo mwezi wa Sebati, chaka chachiwiri cha Dariusi, mau a Yehova anadza kwa Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido mneneri, ndi kuti, Ndinaona usiku, taonani, munthu woyenda pa kavalo wofiira, alikuima pakati pa mitengo yamchisu inali kunsi; ndi pambuyo pake panali akavalo ofiira, odera ndi oyera. Pamenepo ndinati, Awa ndi chinai, mbuyanga? Ndi mthenga wakulankhula ndi ine anati kwa ine, Ndidzakuonetsa awa ndi chiyani. Ndipo wakuima pakati pa mitengo yamchisu anayankha, nati, Awa ndiwo amene Yehova anawatumiza ayendeyende m'dziko. Ndipo iwo anamyankha mthenga wa Yehova wakuima pakati pa mitengo yamchisu, nati, Tayendayenda m'dziko, ndipo taonani, dziko lonse likhala chete, lipumula. Ndipo mthenga wa Yehova anayankha nati, Yehova wa makamu, mudzakhala mpaka liti osachitira chifundo Yerusalemu, ndi midzi ya Yuda, imene munakwiya nayo zaka izi makumi asanu ndi awiri? Ndipo Yehova anamyankha mthenga wakulankhula ndi ine mau okoma, mau akutonthoza mtima. Ndipo mthenga wakulankhula ndi ine anati kwa ine, fuula, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu: Ndichitira nsanje Yerusalemu ndi Ziyoni ndi nsanje yaikulu. Ndipo ndikwiya nao amitundu okhala osatekeseka ndi mkwiyo waukulu; pakuti ndinakwiya pang'ono, ndipo anathandizira choipa. Chifukwa chake atero Yehova: Ndabwera kudza ku Yerusalemu ndi zachifundo; nyumba yanga idzamangidwamo, atero Yehova wa makamu, ndipo adzayesa Yerusalemu ndi chingwe. Fuulanso, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu: Midzi yanga idzalemerera ndi kufalikiranso; ndipo Yehova adzasangalatsanso Ziyoni, nadzasankhamo Yerusalemu. Ndipo ndinakweza maso anga, ndinapenya, taonani, nyanga zinai. Ndipo ndinati kwa mthenga wakulankhula ndi ine, Izi nziyani? Ndipo anandiyankha, Izi ndi nyangazi zinabalalitsa Yuda, Israele, ndi Yerusalemu. Ndipo Yehova anandionetsa osula anai. Pamenepo ndinati, Adzeranji awa? Ndipo ananena, nati, Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda, wopandanso wina woweramutsa mutu wake; koma awa anadza kuziopsa, kugwetsa nyanga za amitundu, amene anakwezera dziko la Yuda nyanga zao kulimwaza. Ndinakwezanso maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, munthu ndi chingwe choyesera m'dzanja lake. Ndipo ndinati, Upita kuti? Ndipo anati kwa ine, Kukayesa Yerusalemu, kuona ngati chitando chake nchotani, ndi m'litali mwake motani. Ndipo taonani, mthenga wolankhula nane anatuluka, ndi mthenga wina anatuluka kukomana naye, nanena naye, Thamanga, lankhula ndi mnyamata uyu, ndi kuti, M'Yerusalemu mudzakhala anthu ngati m'midzi yopanda malinga, chifukwa cha kuchuluka anthu ndi zoweta momwemo. Pakuti Ine, ati Yehova, ndidzakhala kwa iye linga lamoto pozungulira pake, ndipo ndidzakhala ulemerero m'kati mwake. Haya, haya, thawani kudziko la kumpoto ati Yehova; pakuti ndinakubalalitsani ngati mphepo zinai za kuthambo, ati Yehova. Haya Ziyoni, thawa iwe wakukhala ndi mwana wamkazi wa Babiloni. Pakuti atero Yehova wa makamu: Utatha ulemererowo ananditumiza kwa amitundu amene anakufunkhani; pakuti iye wokhudza inu, akhudza mwana wa m'diso lake. Pakuti, taonani, ndidzawayambasira dzanja langa, ndipo adzakhala zofunkha za iwo amene anawatumikira; ndipo mudzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma. Imba, nukondwere, mwana wamkazi wa Ziyoni; pakuti taonani, ndilinkudza, ndipo ndidzakhala pakati pako, ati Yehova. Ndipo amitundu ambiri adzaphatikidwa kwa Yehova tsiku ilo, nadzakhala anthu anga; ndipo ndidzakhala pakati pako, ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma kwa iwe. Ndipo Yehova adzalandira cholowa chake Yuda, ngati gawo lake m'dziko lopatulikalo, nadzasankhanso Yerusalemu. Khalani chete, anthu onse, pamaso pa Yehova; pakuti wagalamuka mokhalira mwake mopatulika. Pamenepo anandionetsa Yoswa mkulu wa ansembe alikuima pamaso pa mthenga wa Yehova, ndi Satana alikuima pa dzanja lake lamanja, atsutsana naye. Ndipo Yehova anati kwa Satana, Yehova akudzudzula, Satana iwe; inde Yehova amene anasankha Yerusalemu akudzudzula; uyu sindiye muuni wofumulidwa kumoto? Koma Yoswa analikuvala nsalu zonyansa naima pamaso pa mthenga. Ndipo Iye anayankha nanena ndi iwo akuima pamaso pake, ndi kuti, Mumvule nsalu zonyansazi. Nati kwa iye, Taona, ndakuchotsera mphulupulu zako, ndipo ndidzakuveka zovala za mtengo wake. Ndipo ndinati, Amuike nduwira yoyera pamutu pake. Naika nduwira yoyera pamutu pake, namveka ndi zovala; ndi mthenga wa Yehova anaimirirapo. Ndipo mthenga wa Yehova anamchitira Yoswa umboni, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu: Ukadzayenda m'njira zanga, ndi kusunga udikiro wanga, pamenepo udzaweruza nyumba yanga, ndi kusunga mabwalo anga, ndipo ndidzakupatsa malo oyendamo mwa awa oimirirapo. Tamvera tsono, Yoswa mkulu wa ansembe, iwe ndi anzako akukhala pansi pamaso pako; pakuti iwo ndiwo chizindikiro; pakuti taonani, ndidzafikitsa mtumiki wanga, ndiye Mphukira. Pakuti taona mwalawo ndinauika pamaso pa Yoswa; pa mwala umodzi pali maso asanu ndi awiri; taonani, ndidzalocha malochedwe ake, ati Yehova wa makamu, ndipo ndidzachotsa mphulupulu ya dziko lija tsiku limodzi. Tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, mudzaitanizana yense mnansi wake patsinde pa mpesa ndi patsinde pa mkuyu. Ndipo mthengayo adalankhula nane, anadzanso, nandiutsa ngati munthu woutsidwa m'tulo take. Ndipo anati kwa ine, Uona chiyani? Ndipo ndinati, Ndaona, taonani, choikapo nyali cha golide yekhayekha, ndi mbale yake pamwamba pake, ndi nyali zake zisanu ndi ziwiri pamenepo; nyalizo zinali ndi misiwe isanu ndi iwiri, ndiyo ya nyalizo zinali pamwamba pake; ndi mitengo iwiri ya azitona pomwepo, wina kudzanja lamanja la mbaleyo, ndi wina kudzanja lake lamanzere. Ndipo ndinayankha ndi kunena ndi mthenga wakulankhula ndi ine, ndi kuti, Izi nziyani mbuyanga? Ndipo mthenga wakulankhula ndi ine anayankha, nati kwa ine, Sudziwa kodi kuti nziyani izi? Ndipo ndinati, Iai, mbuyanga. Pamenepo anayankha, nanena kwa ine, ndi kuti, Awa ndi mau a Yehova kwa Zerubabele, Ndi khamu la nkhondo ai, ndi mphamvu ai, koma ndi Mzimu wanga, ati Yehova wa makamu. Ndiwe yani, phiri lalikulu iwe? Pamaso pa Zerubabele udzasanduka chidikha; ndipo adzatulutsa mwala woikidwa pamwamba, ndi kufuula, Chisomo, chisomo nao. Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, ndi kuti, Manja a Zerubabele anaika maziko a nyumba iyi, manja ake omwe adzaitsiriza; ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma kwa inu. Pakuti wapeputsa tsiku la tinthu tating'ono ndani? Pakuti adzakondwera, asanu ndi awiri awa, nadzaona chingwe cholungamitsira chilili m'dzanja la Zerubabele, ndiwo maso a Yehova; ayendayenda mwa dziko lonse. Pamenepo ndinayankha, ndinati kwa iye, Mitengo iyi iwiri ya azitona kulamanja ndi kulamanzere kwa choikapo nyali nchiyani? Ndipo ndinayankha kachiwiri, ndinati naye, Nzotani nthambi ziwiri izi za azitona zilikutsanula zokha mafuta onga golide mwa misiwe iwiri yagolide? Ndipo anandiyankha, nati, Sudziwa kodi kuti nziyani izi? Ndipo ndinati, Iai, mbuyanga. Pamenepo anati, Awa ndi ana amuna awiri a mafuta oimirira pamaso pa Mbuye wa dziko lonse lapansi. Pamenepo ndinakwezanso maso anga, ndinapenya, taonani, mpukutu wouluka. Ndipo anati kwa ine, Uona chiyani? Ndipo ndinayankha, Ndiona mpukutu wouluka; utali wake mikono makumi awiri, ndi chitando chake mikono khumi. Ndipo anati kwa ine, Ili ndi temberero lilikutulukira pa dziko lonse; pakuti aliyense wakuba adzapirikitsidwa kuno monga mwa ili; ndi aliyense wakulumbira zonama adzapirikitsidwa kuno monga mwa ili. Ndidzalitulutsa ili, ati Yehova wa makamu, ndipo lidzalowa m'nyumba ya wakuba, ndi m'nyumba ya iye wolumbira monama pa dzina langa; ndipo lidzakhala pakati pa nyumba yake, ndi kuitha pamodzi ndi mitengo yake ndi miyala yake. Pamenepo mthenga wakulankhula ndi ine anatuluka, nati kwa ine, Kwezatu maso ako, nuone ngati nchiyani ichi chilikutulukachi. Ndipo ndinati, Nchiyani ichi? Nati iye, Ichi ndi efa alikutuluka. Natinso, Ichi ndi maonekedwe ao m'dziko lonse; ndipo taonani, chozunguniza chantovu chotukulidwa: ndipo ichi ndi mkazi wokhala pakati pa efa. Ndipo anati, Uyu ndi uchimo; namgwetsa m'kati mwa efa; naponya ntovu wolemerawo pakamwa pake. Pamenepo ndinakweza maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, anatuluka akazi awiri, ndi m'mapiko mwao munali mphepo; ndipo anali nao mapiko ngati mapiko a chumba, nanyamula efayo pakati pa dziko ndi thambo. Ndipo ndinati kwa mthenga wakulankhula ndi ine, Amenewa amuka naye kuti efayo? Ndipo anati kwa ine, Kummangira nyumba m'dziko la Sinara; kuti amuike efayo, namkhazikeko pa malo kwake. Ndipo ndinakwezanso maso anga, ndinapenya, ndipo taonani, anatuluka magaleta anai pakati pa mapiri awiri; ndi mapiriwo ndiwo mapiri amkuwa. Ku galeta woyamba kunali akavalo ofiira; ndi kugaleta wachiwiri akavalo akuda; ndi kugaleta wachitatu a kavalo oyera; ndi kugaleta wachinai akavalo olimba amawanga. Ndipo ndinayankha ndinati kwa mthenga wolankhula ndi ine, Izi nziyani, mbuyanga? Ndi mthenga anayankha, nati kwa ine, Izi ndi mphepo zinai zakumwamba zakutuluka kumene zimaimirira pamaso pa Ambuye wa dziko lonse lapansi. Galeta wa akavalo akuda atulukira kudziko la kumpoto; ndi oyerawo atulukira kuwatsata; ndi amawanga atulukira kudziko la kumwera. Ndi amphamvuwo anatuluka nayesa kunka kuyendayenda m'dziko; pakuti adati, Mukani, yendayendani m'dziko. Momwemo anayendayenda m'dziko. Ndipo anandiitana, nanena nane, kuti, Taonani, iwo akutuluka kunka kudziko la kumpoto anapumulitsa Mzimu wanga m'dziko la kumpoto. Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, ndi kuti, Tenga a iwo a kundende, a Helidai, a Tobiya, ndi a Yedaya; nudze tsiku lomwelo, nulowe kunyumba ya Yosiya, mwana wa Zefaniya, kumene anafikirako kuchokera ku Babiloni, ndipo utenge siliva ndi golide, nupange akorona, nuwaike pamutu pa Yoswa mwana wa Yehozadaki mkulu wa ansembe; nunene naye, kuti, Atero Yehova wa makamu, ndi kuti, Taonani, munthu dzina lake ndilo Mphukira, ndipo adzaphuka m'malo mwake, nadzamanga Kachisi wa Yehova: inde adzamanga Kachisi wa Yehova; nadzasenza ulemererowo, nadzakhala ndi kulamulira pa mpando wachifumu wake; nadzakhala wansembe pampando wachifumu wake; ndi uphungu wa mtendere udzakhala pakati pa iwo awiri. Ndipo akorona adzakhala wa Helidai, ndi wa Tobiya, ndi wa Yedaya, ndi wa Heni mwana wa Zefaniya, akhale chikumbutso m'Kachisi wa Yehova. Ndipo iwo akukhala kutali adzafika, nadzamanga ku Kachisi wa Yehova, ndipo inu mudzadziwa kuti Yehova wa makamu ananditumiza kwa inu. Ndipo ichi chidzachitika ngati mudzamvera mwachangu mau a Yehova Mulungu wanu. Ndipo kunachitika chaka chachinai cha mfumu Dariusi, mau a Yehova anadza kwa Zekariya tsiku lachinai la mwezi wachisanu ndi chinai, ndiwo Kisilevi. Ndipo a ku Betele anatuma Sarezere ndi Regemumeleke ndi anthu ao, apepeze Yehova, nanene kwa ansembe a nyumba ya Yehova wa makamu, ndi kwa aneneri, ndi kuti, Kodi ndilire mwezi wachisanu, ndi kudzipatula, monga umo ndikachitira zaka izi zambiri? Ndipo mau a Yehova wa makamu anadza kwa ine, ndi kuti, Nena kwa anthu onse a m'dziko, ndi kwa ansembe, kuti, Muja mukasala ndi kulira mwezi wachisanu, ndi wachisanu ndi chitatu, zaka izi makumi asanu ndi awiri, kodi mukasalira Ine, Inedi? Ndipo pamene mukadya si ndinu, mukamwa si ndinu kodi? Si ndiwo mau Yehova anawalalikira mwa aneneri oyamba aja, muja Yerusalemu anali nao okhalamo, ndi wokhazikika; ndi m'midzi mwake pozungulira pake, ndi m'dziko la kumwera, ndi m'chidikha munali anthu okhalamo? Ndipo mau a Yehova anadza kwa Zekariya, ndi kuti, Watero Yehova wa makamu, kuti, Weruzani chiweruzo choona, nimuchitire yense mnzake chifundo ndi ukoma mtima; musazunza mkazi wamasiye, kapena ana amasiye, mlendo kapena waumphawi; ndipo nnena mmodzi wa inu alingirire m'mtima mwake kumchitira choipa munthu mnzake. Koma anakana kumvera, nakaniza phewa lao, natseka makutu ao, kuti asamve. Inde, anasanduliza mitima yao ikhale ngati mwala woti gwa, kuti angamve chilamulo, ndi mau amene Yehova wa makamu anatumiza ndi Mzimu wake mwa aneneri oyamba aja; m'menemo munafuma mkwiyo waukulu wochokera kwa Yehova wa makamu. Ndipo kunachitika, monga Iye anafuula, koma iwo sanamvere; momwemo iwo adzafuula, koma Ine sindidzamva, ati Yehova wa makamu; koma ndidzawabalalitsa ndi kamvulumvulu mwa amitundu onse amene sanawadziwe. Motero dziko linakhala bwinja, m'mbuyo mwao; palibe munthu wopitapo ndi kubwererako; pakuti adaika dziko lofunikalo labwinja. Ndipo mau a Yehova wa makamu anadza kwa ine, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu: Ndimchitira nsanje Ziyoni ndi nsanje yaikulu, ndipo ndimchitira nsanje ndi ukali waukulu. Atero Yehova: Ndabwerera kudza ku Ziyoni, ndidzakhala pakati pa Yerusalemu; ndi Yerusalemu adzatchedwa, Mudzi wa choonadi; ndi phiri la Yehova wa makamu, Phiri lopatulika. Atero Yehova wa makamu: M'miseu ya Yerusalemu mudzakhalanso amuna ndi akazi okalamba, yense ndi ndodo yake m'dzanja lake chifukwa cha ukalamba wake. Ndi m'miseu ya mudzi mudzakhala ana aamuna ndi aakazi akusewera m'miseu yake. Atero Yehova wa makamu: Chikakhala chodabwitsa pamaso pa otsala a anthu awa masiku awo, kodi chidzakhalanso chodabwitsa pamaso panga? Ati Yehova wa makamu. Atero Yehova wa makamu: Taonani, ndidzapulumutsa anthu anga m'dziko la kum'mawa, ndi m'dziko la kumadzulo; ndipo ndidzabwera nao, nadzakhala m'kati mwa Yerusalemu; ndipo iwo adzakhala anthu anga, nanenanso ndidzakhala Mulungu wao, m'choonadi ndi m'chilungamo. Atero Yehova wa makamu: Alimbike manja anu, inu akumva masiku ano mau awa pakamwa pa aneneri amene anakhalako tsiku lakuikidwa maziko a nyumba ya Yehova wa makamu, ndiyo Kachisi, kuti amangidwe. Pakuti asanafike masiku aja, panalibe kulipidwira munthu, kapena kulipidwira nyama, ndipo analibe mtendere iye wakutuluka, kapena wakulowa, chifukwa cha wosautsa; pakuti ndinatumiza munthu yense atsutsane naye mnzake. Koma tsopano sindidzakhala kwa otsala a anthu awa monga momwe ndinakhalira masiku oyamba, ati Yehova wa makamu. Pakuti padzakhala mbeu ya mtendere; mpesa udzapatsa zipatso zake, ndi nthaka idzapatsa zobala zake, ndi miyamba idzapata mame ao; ndipo ndidzalandiritsa otsala a anthu awa izi zonse, chikhale cholowa chao. Ndipo kudzachitika kuti, monga munali chotembereretsa mwa amitundu, inu nyumba ya Yuda, ndi nyumba ya Israele, momwemo ndidzakusungani, ndipo mudzakhala chodalitsa nacho; musaope, alimbike manja anu. Pakuti atero Yehova wa makamu: Monga ndinalingirira kuchitira inu choipa, muja makolo anu anautsa mkwiyo wanga, ati Yehova wa makamu, ndipo sindinawaleka; momwemonso ndinalingirira masiku ano kuchitira chokoma Yerusalemu ndi nyumba ya Yuda; musaopa. Izi ndizo muzichite: Nenani choonadi yense ndi mnzake; weruzani zoona ndi chiweruzo cha mtendere m'zipata zanu; ndipo musalingirira choipa m'mtima mwanu yense pa mnzake; nimusakonde lumbiro lonama; pakuti izi zonse ndidana nazo, ati Yehova. Ndipo mau a Yehova wa makamu anadza kwa ine, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu: Kusala kwa mwezi wachinai, ndi kusala kwa mwezi wachisanu, ndi kusala kwa mwezi wachisanu ndi chiwiri, ndi kusala kwa mwezi wakhumi kukhale kwa nyumba ya Yuda chimwemwe ndi chikondwerero, ndi nyengo zoikika zosekerera; chifukwa chake kondani choonadi ndi mtendere. Atero Yehova wa makamu: Kudzachitikanso kuti mitundu ya anthu, ndi okhalamo m'midzi yambiri adzafika, ndi okhala m'mudzi umodzi adzamuka kumudzi wina, ndi kuti, Tiyeni msanga kukapepeza Yehova, ndi kufunafuna Yehova wa makamu; ndimuka inenso. Inde, mitundu yambiri ya anthu, ndi amitundu amphamvu adzadza kufunafuna Yehova wa makamu m'Yerusalemu, ndi kupepeza Yehova. Atero Yehova wa makamu: Kudzachitika masiku awo amuna khumi adzagwira, ndiwo a manenedwe onse a amitundu, inde adzagwira mkawo wa munthu ali Myuda, ndi kuti, Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu. Katundu wa mau a Yehova pa dziko la Hadaraki, ndipo Damasiko adzakhala popumula pake; pakuti Yehova apenyerera anthu monga apenyerera mafuko onse a Israele; ndi Hamati yemwe wogundana naye malire; Tiro ndi Sidoni, angakhale ali ndi nzeru zambiri. Ndipo Tiro adzadzimangira polimbikirapo, nadzakundika siliva ngati fumbi, ndi golide woyenga ngati thope la kubwalo. Taonani, Yehova adzamlanda zake, nadzakantha mphamvu yake igwe m'manja; ndipo adzatha ndi moto. Asikeloni adzachiona, nadzaopa; Gazanso, nadzanjenjemera kwambiri; ndi Ekeroni, pakuti chiyembekezo chake chachitidwa manyazi; ndipo mfumu idzataika ku Gaza, ndi Asikeloni adzasowa okhalamo. Ndi mtundu wa anthu osokonezeka udzakhala m'Asidodi, ndipo ndidzaononga kudzikuza kwa Afilisti. Ndipo ndidzachotsa mwazi wake m'kamwa mwake, ndi zonyansa zake pakati pa mano ake; momwemo iyenso adzakhala wotsalira wa Mulungu wathu, ndipo adzakhala ngati mkulu wa fuko m'Yuda, ndi Ekeroni ngati Myebusi. Ndipo ndidzamangira nyumba yanga misasa, kuiletsera nkhondo, asapitepo munthu kapena kubweranso; ndipo wakuwasautsa sadzapitanso pakati pao; pakuti tsopano ndapenya ndi maso anga. Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; wofatsa ndi wokwera pa bulu, ndi mwana wamphongo wa bulu. Ndipo ndidzaononga magaleta kuwachotsa m'Efuremu, ndi akavalo kuwachotsa m'Yerusalemu; ndi uta wa nkhondo udzaonongeka; ndipo adzanena zamtendere kwa amitundu; ndi ufumu wake udzakhala kuyambira kunyanja kufikira nyanja, ndi kuyambira ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko. Iwenso, chifukwa cha mwazi wa pangano lako ndinatulutsa andende ako m'dzenje m'mene mulibe madzi. Bwererani kudza kulinga, andende a chiyembekezo inu; ngakhale lero lino ndilalikira kuti ndidzakubwezera chowirikiza. Pakuti ndadzikokera Yuda, ndadzaza uta ndi Efuremu; ndipo ndidzautsa ana ako, Ziyoni, alimbane nao ana ako, Yavani, ndipo ndidzakuyesa lupanga la ngwazi. Ndipo Yehova adzaoneka pamwamba pao, ndi muvi wake udzatuluka ngati mphezi; ndipo Ambuye Mulungu adzaomba lipenga, nadzayenda ndi akavumbulu a kumwera. Yehova wa makamu adzawatchinjiriza; ndipo adzadza, nadzapondereza miyala yoponyera; ndipo adzamva, nadzachita phokoso ngati avinyo; ndipo adzadzazidwa ngati mbale, ngati ngodya za guwa la nsembe. Ndipo Yehova Mulungu wao adzawapulumutsa tsiku ilo, ngati zoweta za anthu ake; pakuti adzakhala ngati miyala ya m'korona yakunyezimira pa dziko lake. Pakuti ukoma wake ndi waukulu ndithu, ndi kukongola kwake nkwakukulu ndithu! Tirigu adzakometsera anyamata, ndi vinyo watsopano anamwali. Pemphani kwa Yehova mvula, m'nyengo ya mvula ya masika, kwa Yehova wolenga mphezi; ndipo adzawapatsa mivumbi ya mvula, kwa yense zophukira kuthengo. Pakuti aterafi anena zopanda pake, ndi aula aona bodza; nafotokoza maloto achabe, asangalatsa nazo zopanda pake; chifukwa chake ayendayenda ngati nkhosa, azunzika popeza palibe mbusa. Mkwiyo wanga wayakira abusa, ndipo ndidzalanga atonde; pakuti Yehova wa makamu adzazonda zoweta zake, ndizo nyumba ya Yuda, nadzaziika ngati kavalo wake waulemerero kunkhondo. Kwa iye kudzafuma mwala wa kungodya, kwa iye msomali, kwa iye uta wankhondo, kwa iye osautsa onse pamodzi. Ndipo adzakhala ngati ngwazi zakupondereza adani m'thope la kubwalo kunkhondo; ndipo adzachita nkhondo, chifukwa Yehova ali nao; ndi apakavalo adzachitidwa manyazi. Ndipo ndidzalimbitsa nyumba ya Yuda, ndi kusunga nyumba ya Yosefe, ndipo ndidzawakhalitsa, pakuti ndawachitira chifundo; ndipo adzakhala monga ngati sindinawataya konse; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, ndipo ndidzawamvera. Ndipo iwo a ku Efuremu adzakhala ngati ngwazi, ndi mtima wao udzakondwera ngati ndi vinyo; ndipo ana ao adzachiona nadzakondwera; mtima wao udzakondwerera mwa Yehova. Ndidzawaimbira mluzu ndi kuwasonkhanitsa, pakuti ndawaombola; ndipo adzachuluka monga anachulukira kale. Ndipo ndidzawafesa mwa mitundu ya anthu, ndipo adzandikumbukira m'maiko akutali; nadzakhala pamodzi ndi ana ao, nadzabwera. Ndidzawatenganso kudziko la Ejipito, ndi kuwasonkhanitsa m'Asiriya; ndipo ndidzalowa nao m'dziko la Giliyadi ndi Lebanoni; koma sadzawafikira. Ndipo adzapita pakati pa nyanja ya nsautso, nadzapanda mafunde a m'nyanja, ndi maiwe onse a mtsinje adzaphwa; ndi kudzikuza kwa Asiriya kudzagwetsedwa; ndi ndodo yachifumu ya Ejipito idzachoka. Ndipo ndidzawalimbitsa mwa Yehova; ndipo adzayendayenda m'dzina lake; ati Yehova. Tsegula pa makomo ako Lebanoni, kuti moto uthe mikungudza yako. Chema, mtengo wamlombwa, pakuti mkungudza wagwa, popeza mitengo yokoma yaipitsidwa; chemani athundu a ku Basani, pakuti nkhalango yotchinjirizika yagwa pansi. Mau a kuchema kwa abusa! Pakuti ulemerero wao waipsidwa; mau a kubangula kwa misona ya mikango! Pakuti kudzikuza kwa Yordani kwaipsidwa. Atero Yehova Mulungu wanga: Dyetsani zoweta zakukaphedwa; zimene eni ake azipha, nadziyesera osapalamula; ndi iwo akuwagulitsa akuti, Alemekezedwe Yehova, pakuti ine ndine wolemera; ndi abusa ao sazichitira chifundo. Pakuti sindidzachitiranso chifundo okhala m'dzikomo, ati Yehova; koma taonani, ndidzapereka anthu, yense m'dzanja la mnansi wake, ndi m'dzanja la mfumu yake; ndipo iwo adzakantha dzikoli, ndi m'dzanja mwao sindidzawalanditsa. M'mwemo ndinadyetsa zoweta zakukaphedwa, ndizo zoweta zonyankhalala. Ndipo ndinadzitengera ndodo ziwiri; ina ndinaitcha Chisomo, inzake ndinaitcha Chomanganitsa; ndipo ndinadyetsa zowetazo. Ndipo ndinatha abusa atatuwo mwezi umodzi; pakuti mtima wanga unalema nao, ndi mtima waonso unaipidwa nane. Pamenepo ndinati, Sindidzadyetsanso inu; chilikufa chife; chosoweka chisoweke; ndi zotsala zidyane, chonse nyama ya chinzake. Ndipo ndinatenga ndodo yanga Chisomo, ndi kuidula pakati, kuti ndiphwanye pangano langa ndinalichita ndi mitundu yonse ya anthu. Ndipo linathyoka tsikulo, momwemo zonyankhalala za zoweta, zakundisamalira Ine, zinadziwa kuti ndiwo mau a Yehova. Ndipo ndinanena nao, Chikakomera inu, ndipatseni mphotho yanga; ngati iai, lekani. Ndipo anayesa mphotho yanga, kulemera kwake masekeli a siliva makumi atatu. Ndipo Yehova anati kwa ine, Kaziponye kwa woumba mbiya, mtengo wake wokometsetsa anandiyesawo. Ndipo ndinatenga masekeli makumi atatu a siliva, ndi kuziponya kwa woumba mbiya, m'nyumba ya Yehova. Pamenepo ndinadula ndodo yanga ina, ndiyo Chomanganitsa, kuti ndithetse chibale cha pakati pa Yuda ndi Israele. Ndipo Yehova anati kwa ine, Dzitengerenso zipangizo za mbusa wopusa. Pakuti taonani, ndidzautsa mbusa m'dziko amene sadzazonda otayika, kapena kufunafuna zomwazika, kapena kulunzitsa yothyoka, kapena kudyetsa yamoyo, koma adzadya nyama ya zonenepa, nadzang'amba ziboda zao. Tsoka mbusa wopanda pake, wakusiya zoweta! Lupanga pa dzanja lake, ndi pa diso lake la kumanja; dzanja lake lidzauma konse, ndi diso lake lamanja lidzada bii. Katundu wa mau a Yehova wakunena Israele. Atero Yehova, wakuyala miyamba, ndi kuika maziko a dziko lapansi, ndi kulenga mzimu wa munthu m'kati mwake; Taonani, ndidzaika Yerusalemu akhale chipanda chodzandiritsa kwa mitundu yonse ya anthu yozungulirapo, ndipo chidzafikira Yuda yemwe pomangira misasa Yerusalemu. Ndipo kudzachitika tsiku ilo, ndidzaika Yerusalemu akhale mwala wolemetsa mitundu yonse ya anthu; onse akuusenza adzadzilasa nao; ndi amitundu onse a pa dziko lapansi adzasonkhana kutsutsana nao. Tsiku ilo, ati Yehova, ndidzakantha kavalo aliyense ndi kumdabwitsa, ndi womkwera adzayaluka; ndipo ndidzatsegulira maso anga nyumba ya Yuda, ndi kukantha kavalo aliyense wa mitundu ya anthu akhale wakhungu. Ndipo akalonga a Yuda adzanena m'mtima mwao, Okhala m'Yerusalemu ndiwo mphamvu yanga m'Yehova wa makamu Mulungu wao. Tsiku ilo ndidzaika akalonga a Yuda ngati phale la moto pansi pa nkhuni, ndi ngati muuni wamoto mwa mitolo ya tirigu; ndipo adzatha mitundu yonse ya anthu pozungulirapo, kudzanja lamanja ndi lamanzere; ndipo Yerusalemu adzakhalanso m'malo mwake, m'Yerusalemu. Ndipo Yehova adzayamba kupulumutsa mahema a Yuda, kuti ulemerero wa nyumba ya Davide ndi ulemerero wa okhala m'Yerusalemu usakulire Yuda. Tsiku ilo Yehova adzatchinjiriza okhala m'Yerusalemu; ndi iye wokhumudwa pakati pao tsiku lomwelo adzakhala ngati Davide; ndi nyumba ya Davide idzakhala ngati Mulungu, ngati mthenga wa Yehova pakati pao. Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ndidzayesa kuononga amitundu onse akudza kuyambana ndi Yerusalemu. Ndipo ndidzatsanulira pa nyumba ya Davide, ndi pa okhala m'Yerusalemu, mzimu wa chisomo ndi wakupembedza; ndipo adzandipenyera Ine amene anandipyoza; nadzamlira ngati munthu alira mwana wake mmodzi yekha, nadzammvera zowawa mtima, monga munthu amvera zowawa mtima mwana wake woyamba. Tsiku lomwelo kudzakhala maliro akulu m'Yerusalemu, ngati maliro a Hadadirimoni m'chigwa cha Megido. Ndipo dziko lidzalira, banja lililonse pa lokha; banja la nyumba ya Davide pa lokha, ndi akazi ao pa okha; banja la nyumba ya Natani pa lokha, ndi akazi ao pa okha; banja la nyumba ya Levi pa lokha, ndi akazi ao pa lokha; banja la Asimei pa okha, ndi akazi ao pa okha; mabanja onse otsala, banja lililonse pa lokha, ndi akazi ao pa okha. Tsiku lomwelo padzatsegukira nyumba ya Davide ndi okhala m'Yerusalemu kasupe wa kwa uchimo ndi chidetso. Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, ndidzaononga maina a mafano m'dziko; ndipo sadzakumbukikanso; ndipo ndidzachotsa m'dziko aneneri ndi mzimu wachidetso. Ndipo kudzachitika, akaneneranso wina, atate wake ndi mai wake ombala adzanena naye, Sudzakhala ndi moyo, pakuti unena bodza m'dzina la Yehova; ndipo atate wake ndi mai wake ombala adzamgwaza ponenera iye. Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo kuti aneneri adzachita manyazi yense ndi masomphenya ake, ponenera iye; ndipo sadzavala chofunda chaubweya kunyenga nacho; koma adzati, Sindili mneneri, ndili wolima munda; pakuti munthu anandiyesa kapolo kuyambira ubwana wanga. Ndipo wina akati kwa iye, Zipsera izi m'manja mwako nza chiyani? Adzayankha, Ndizo za mabala anandilasa m'nyumba ya ondikonda. Galamuka, lupanga, pa mbusa wanga, ndi pa munthu mnzanga wa pamtima, ati Yehova wa makamu; kantha mbusa, ndi nkhosa zidzabalalika; koma ndidzabwezera dzanja langa pa zazing'onozo. Ndipo kudzachitika m'dziko lonse, ati Yehova, magawo awiri m'menemo adzalikhidwa nadzafa; koma gawo lachitatu lidzasiyidwa m'mwemo. Ndi gawo lachitatulo ndidzalitengera kumoto, ndi kuwayenga ngati ayenga siliva, ndi kuwayesa monga ayesa golide; adzaitana dzina langa, ndipo ndidzawamvera; ndidzati, Awa ndi anthu anga; ndi iwo adzati, Yehova ndi Mulungu wanga. Taonani likudza tsiku la Yehova, limene zofunkha zako zidzagawanika pakati pako. Pakuti ndidzasonkhanitsa amitundu onse alimbane ndi Yerusalemu; ndipo mudziwo udzalandidwa, ndi nyumba zidzafunkhidwa, ndi akazi adzakakamizidwa; ndi limodzi la magawo awiri la mudzi lidzatuluka kunka kundende, koma anthu otsala sadzaonongeka m'mudzimo. Pamenepo Yehova adzatuluka, nadzachita nkhondo ndi amitundu aja, monga anachitira nkhondo tsiku lakudumana. Ndi mapazi ake adzaponda tsiku lomwelo pa phiri la Azitona, lili pandunji pa Yerusalemu kum'mawa, ndi phiri la Azitona lidzang'ambika pakati kuloza kum'mawa ndi kumadzulo, ndipo padzakhala chigwa chachikulu; ndi gawo lina la phirilo lidzamuka kumpoto, ndi gawo lina kumwera. Pamenepo mudzathawa kudzera chigwa cha mapiri anga; pakuti chigwa cha mapiri chidzafikira ku Azali; ndipo mudzathawa monga umo munathawira chivomezi, masiku a Uziya mfumu ya Yuda; ndipo Yehova Mulungu wanga adzadza, ndi opatulika onse pamodzi ndi Inu. Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, sikudzakhala kuunika, zowalazo zidzada; koma lidzakhala tsiku la pa lokha lodziwika ndi Yehova; palibe usana, palibe usiku; koma kudzatero kuti madzulo kudzati mbee. Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo kuti madzi amoyo adzatuluka ku Yerusalemu; gawo lao lina kunka ku nyanja ya kum'mawa, ndi gawo lina kunka ku nyanja ya kumadzulo; adzatero nyengo ya dzinja ndi ya mwamvu. Ndipo Yehova adzakhala mfumu ya dziko lonse; tsiku lomwelo Yehova adzakhala Iye yekha, ndi dzina lake ilo lokha. Dziko lonse lidzasandulika, lidzanga chidikha, kuyambira ku Geba kufikira ku Rimoni, kumwera kwa Yerusalemu; ndipo pali uwupo padzakhala ponyamuka, ndipo udzakhala m'malo mwake, kuyambira ku chipata cha Benjamini kufikira ku malo a chipata choyamba, kufikira ku chipata cha kungodya, ndi kuyambira nsanja ya Hananele kufikira ku zoponderamo mphesa za mfumu. Ndipo anthu adzakhala m'menemo, ndipo sipadzakhalanso kuonongetsa; koma Yerusalemu adzakhala mosatekeseka. Ndipo mliri umene Yehova adzakantha nao mitundu yonse ya anthu imene idathira nkhondo pa Yerusalemu ndi uwu: nyama yao idzaonda akali chilili pa mapazi ao, ndi maso ao adzapuwala m'funkha mwao, ndi lilime lao lidzanyala m'kamwa mwao. Ndipo kudzali tsiku lomwelo, kuti chisokonezo chachikulu chochokera kwa Yehova chidzakhala pakati pao; ndipo adzagwira yense dzanja la mnzake; ndi dzanja lake lidzaukira dzanja la mnzake. Ndi Yuda yemwe adzachita nkhondo ku Yerusalemu; ndi zolemera za amitundu onse ozungulirapo zidzasonkhanitsidwa, golide, ndi siliva, ndi zovala zambirimbiri. Momwemonso mliri wa pa akavalo, nyuru, ngamira, ndi abulu, ndi nyama zonse zokhala m'misasa iyo, udzakhala ngati mliri uwo. Ndipo kudzachitika kuti otsala onse a amitundu onse anadzawo kulimbana ndi Yerusalemu, adzakwera chaka ndi chaka kulambira mfumu Yehova wa makamu, ndi kusunga chikondwerero cha Misasa. Ndipo kudzachitika kuti aliyense wa mabanja a dziko wosakwera kunka ku Yerusalemu kulambira mfumu Yehova wa makamu, pa iwowa sipadzakhala mvula. Ndipo banja la ku Ejipito likapanda kukwera, losafika, sudzawagwera kodi mliri umene Yehova adzakantha nao amitundu osakwera kusunga chikondwerero cha Misasa? Ili ndi tchimo la Ejipito, ndi tchimo la amitundu onse osakwerako kusunga chikondwerero cha Misasa. Tsiku lomwelo padzaoneka pa miliu ya akavalo Opatulikira Yehova; ndi mbiya za m'nyumba ya Yehova zidzanga mbale za kuguwa la nsembe. Inde mbiya zonse za m'Yerusalemu ndi m'Yuda zidzakhala zopatulikira Yehova wa makamu; ndi onse akuphera nsembe adzafika nadzatengako, ndi kuphikamo; ndipo tsiku lomwelo simudzakhalanso Mkanani m'nyumba ya Yehova wa makamu. Katundu wa mau a Yehova wa kwa Israele mwa Malaki. Ndakukondani, ati Yehova; koma inu mukuti, Mwatikonda motani? Esau si mkulu wake wa Yakobo kodi? Ati Yehova; ndipo ndinakonda Yakobo; koma Esau ndinamuda, ndinasanduliza mapiri ake abwinja, ndi kupereka cholowa chake kwa ankhandwe a m'chipululu. Chinkana Edomu akuti, Taphwanyika, koma tidzabwera ndi kumanganso mabwinja; atero Yehova wa makamu, Adzamanga, koma Ine ndidzapasula; ndipo adzawatcha, Dziko la choipa, ndiponso, Anthu amene Yehova akwiya nao chikwiyire. Ndipo maso anu adzaona, nimudzati, Yehova ali wamkulu kupitirira malire a Israele. Mwana alemekeza atate wake, ndi mnyamata mbuye wake; ngati Ine tsono ndine atate, uli kuti ulemu wanga? Ngati Ine ndine mbuye, kundiopa kuli kuti? Ati Yehova wa makamu kwa inu ansembe akupeputsa dzina langa. Ndipo mukuti, Tapeputsa dzina lanu motani? Mupereka mkate wodetsedwa pa guwa langa la nsembe; ndipo mukuti, Takudetsani motani? M'menemo, mwakuti munena, Gome la Yehova nlonyozeka. Ndipo pamene mupereka yakhungu ikhale nsembe, mukuti, Palibe choipa! Ndi popereka yotsimphina ndi yodwala, palibe choipa! Kaiperekeni kwa kazembe wanu, mudzamkomera kodi? Kapena adzakuvomerezani kodi? Ati Yehova wa makamu. Ndipo tsopano, mupepeze Mulungu, kuti atichitire chifundo; ichicho chichokera kwa inu; kodi Iye adzavomereza ena a inu? Ati Yehova wa makamu. Mwenzi atakhala wina mwa inu wakutseka pamakomo, kuti musasonkhe moto chabe pa guwa langa la nsembe! Sindikondwera nanu, ati Yehova wa makamu, ndipo sindidzalandira chopereka m'dzanja lanu. Pakuti kuyambira kotulukira dzuwa kufikira kolowera kwake dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu; ndipo m'malo monse adzaperekera dzina langa chofukiza ndi chopereka choona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu, ati Yehova wa makamu. Koma inu muliipsa, pakunena inu, Gome la Yehova laipsidwa, ndi zipatso zake, chakudya chake, chonyozeka. Mukutinso, Taonani, ncholemetsa ichi! Ndipo mwachipeputsa, ati Yehova wa makamu; ndipo mwabwera nazo zofunkha, ndi zotsimphina, ndi zodwala; momwemo mubwera nayo nsembe; kodi ndiyenera kuilandira kudzanja lanu? Ati Yehova. Koma wotembereredwa wonyengayo, wokhala nayo yaimuna m'gulu lake, nawinda, naphera Yehova nsembe chinthu chachilema; pakuti Ine ndine mfumu yaikulu, ati Yehova wa makamu; ndipo dzina langa ndi loopsa pakati pa amitundu. Ndipo tsono, ansembe inu, lamulo ili ndi la kwa inu. Mukapanda kumvera, mukapanda kuliika mumtima mwanu, kupatsa dzina langa ulemerero, ati Yehova wa makamu, ndidzakutumizirani temberero, ndi kutemberera madalitso anu; inde, ndawatemberera kale chifukwa simuliika mumtima. Taonani, ndidzaipsa mbeu chifukwa cha inu, ndi kuwaza ndowe pankhope panu, ndizo ndowe za nsembe zanu, ndipo adzakuchotsani pamodzi nacho. Ndipo mudzadziwa kuti ndatumiza lamulo ili kwa inu, kuti chipangano changa chikhale ndi Levi, ati Yehova wa makamu. Chipangano changa chinali naye cha moyo ndi cha mtendere; ndipo ndinampatsa izi kuti aope; nandiopa, naopsedwa chifukwa cha dzina langa. Chilamulo cha zoona chinali m'kamwa mwake, ndi chosalungama sichinapezeka m'milomo mwake; anayenda nane mumtendere ndi moongoka, nabweza ambiri aleke mphulupulu. Pakuti milomo ya wansembe iyenera kusunga chidziwitso, ndi anthu ayenera kufunafuna chilamulo pakamwa pake; pakuti iye ndiye mthenga wa Yehova wa makamu. Koma inu mwapatuka m'njira; mwakhumudwitsa ambiri m'chilamulo; mwaipsa chipangano cha Levi, ati Yehova wa makamu. Chifukwa chake Inenso ndakuikani onyozeka ndi ochepseka kwa anthu onse, popeza simunasunga njira zanga, koma munaweruza mwankhope pochita chilamulo. Kodi sitili naye Atate mmodzi ife tonse? Sanatilenge kodi Mulungu mmodzi? Tichita monyengezana yense ndi mnzake chifukwa ninji, ndi kuipsa chipangano cha makolo athu? Yuda wachita monyenga, ndi m'Israele ndi m'Yerusalemu mwachitika chonyansa; pakuti Yuda waipsa chipatuliko cha Yehova chimene achikonda, nakwatira mwana wamkazi wa mulungu wachilendo. Yehova adzalikha munthu wakuchita ichi, wogalamutsa ndi wovomereza m'mahema a Yakobo, ndi iye wopereka chopereka kwa Yehova wa makamu. Ndi ichi mubwereza kuchichita: mukuta guwa la nsembe la Yehova ndi misozi, ndi kulira, ndi kuusa moyo; momwemo Iye sasamaliranso chopereka, kapena kulandira mokondwera m'dzanja lanu. Koma mukuti, Chifukwa ninji? Chifukwa kuti Yehova anali mboni pakati pa iwe ndi mkazi wa ubwana wako, amene unamchitira chosakhulupirika, chinkana iye ndiye mnzako, mkazi wa pangano lako. Ndipo sanatero kodi wina womtsalira mzimu? Ndipo winayo anatero bwanji? Anatero pofuna mbeu ya Mulungu. Koma sungani mzimu wanu; ndipo asamchitire monyenga mkazi wa ubwana wake ndi mmodzi yense. Pakuti ndidana nako kuleka kumene, ati Yehova Mulungu wa Israele, ndi iye wakukuta chovala chake ndi chiwawa, ati Yehova wa makamu; chifukwa chake sungani mzimu wanu kuti musachite mosakhulupirika. Mwalemetsa Yehova ndi mau anu. Koma mukuti, Tamlemetsa ndi chiyani? Ndi ichi chakuti munena, Yense wakuchita choipa ali wokoma pamaso pa Mulungu, ndipo akondwera nao; kapena, Ali kuti Mulungu wa chiweruzo? Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu. Koma ndani adzapirira tsiku la kudza kwake? Ndipo adzaima ndani pooneka Iye? Pakuti adzanga moto wa woyenga, ndi sopo wa otsuka; ndipo adzakhala pansi ndi kuyenga ndi kuyeretsa siliva, nadzayeretsa ana a Levi, nadzawayengetsa ngati golide ndi siliva; pamenepo iwo adzapereka kwa Yehova zopereka m'chilungamo. Pamenepo chopereka cha Yuda ndi Yerusalemu chidzakomera Yehova, ngati masiku a kale lija, ndi ngati zaka zoyamba zija. Ndipo ndidzayandikiza kwa inu kuti ndiweruze; ndipo ndidzakhala mboni yakufulumira kutsutsa obwebweta, ndi achigololo, ndi olumbira monama; ndi iwo akunyenga wolembedwa ntchito pa kulipira kwake, akazi amasiye, ndi ana amasiye, ndi wakuipsa mlandu wa mlendo, osandiopa Ine, ati Yehova wa makamu. Pakuti Ine Yehova sindisinthika, chifukwa chake inu ana a Yakobo simunathedwa. Kuyambira masiku a makolo anu mwapatuka kuleka malemba anga osawasunga. Bwererani kudza kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu, ati Yehova wa makamu. Koma inu mukuti, Tibwerere motani? Kodi munthu adzalanda za Mulungu? Ndipo inu mundilanda Ine. Koma mukuti, Takulandani zotani? Limodzilimodzi la magawo khumi, ndi zopereka. Mutembereredwa ndi temberero; pakuti mundilanda Ine, ndinu mtundu uwu wonse. Mubwere nalo limodzilimodzi lonse la khumi, kunyumba yosungiramo, kuti m'nyumba mwanga mukhale chakudya; ndipo mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira. Ndipo ndidzadzudzula zolusa chifukwa cha inu, kuti zisakuonongereni zipatso za nthaka yanu; ngakhale mpesa wanu sudzayoyoka zipatso zake, zosacha m'munda, ati Yehova wa makamu. Ndipo amitundu onse adzatcha inu odala; pakuti mudzakhala dziko lokondweretsa, ati Yehova wa makamu. Mau anu andilimbira, ati Yehova. Koma inu mukuti, Tanena motsutsana nanu ndi chiyani? Mwanena, Kutumikira Mulungu nkwa chabe; ndipo tapindulanji ndi kusunga udikiro wake, ndi kuyenda ovala zamaliro pamaso pa Yehova wa makamu? Ndipo tsopano tiwatcha odzikuza odala, inde iwo ochita zoipa amangidwa ngati nyumba; inde, ayesa Mulungu, napulumuka. Pamenepo iwo akuopa Yehova analankhulana wina ndi mnzake; ndipo Yehova anawatchera khutu namva, ndi buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, la kwa iwo akuopa Yehova, nakumbukira dzina lake. Ndipo adzakhala angaanga, ati Yehova wa makamu, tsiku ndidzaikalo, ndipo ndidzawaleka monga munthu aleka mwana wake womtumikira. Pamenepo mudzabwera ndi kuzindikira pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosamtumikira. Pakuti taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng'anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akuchita choipa. Adzakhala ngati chiputu; ndi tsiku lilinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu, osawasiyira muzu kapena nthambi. Koma inu akuopa dzina langa, dzuwa la chilungamo lidzakutulukirani, muli kuchiritsa m'mapiko mwake; ndipo mudzatuluka ndi kutumphatumpha ngati anaang'ombe onenepa otuluka m'khola. Ndipo mudzapondereza oipa; pakuti adzakhala ngati mapulusa kumapazi anu, tsiku ndidzaikalo, ati Yehova wa makamu. Kumbukirani chilamulo cha Mose mtumiki wanga, ndinamlamuliracho m'Horebu chikhale cha Israele lonse, ndicho malemba ndi maweruzo. Taonani, ndidzakutumizirani Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova. Ndipo adzabwezera mitima ya atate kwa ana, ndi mitima ya ana kwa atate ao; kuti ndisafike ndi kukantha dziko lionongeke konse. Buku la kubadwa kwa Yesu Khristu, mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu. Abrahamu anabala Isaki; ndi Isaki anabala Yakobo; ndi Yakobo anabala Yuda ndi abale ake; ndi Yuda anabala Perezi ndi Zera mwa Tamara; ndi Perezi anabala Hezironi; ndi Hezironi anabala Ramu; ndi Ramu anabala Aminadabu; ndi Aminadabu anabala Nasoni; ndi Nasoni anabala Salimoni; ndi Salimoni anabala Bowazi mwa Rahabu; ndi Bowazi anabala Obede mwa Rute; ndi Obede anabala Yese; ndi Yese anabala Davide mfumuyo. Ndipo Davide anabala Solomoni mwa mkazi wa Uriya; ndi Solomoni anabala Rehobowamu; ndi Rehobowamu anabala Abiya; ndi Abiya anabala Asa; ndi Asa anabala Yehosafati; ndi Yehosafati anabala Yoramu; ndi Yoramu anabala Uziya; ndi Uziya anabala Yotamu; ndi Yotamu anabala Ahazi; ndi Ahazi anabala Hezekiya; ndi Hezekiya anabala Manase; ndi Manase anabala Amoni; ndi Amoni anabala Yosiya; ndi Yosiya anabala Yekoniya ndi abale ake pa nthawi yakutengedwa kunka ku Babiloni. Ndipo pambuyo pake pa kutengedwako ku Babiloni, Yekoniya anabala Sealatiele; ndi Sealatiele anabala Zerubabele; ndi Zerubabele anabala Abihudi; ndi Abihudi anabala Eliyakimu; ndi Eliyakimu anabala Azoro; ndi Azoro anabala Zadoki; ndi Zadoki anabala Akimu; ndi Akimu anabala Eliudi; ndi Eliudi anabala Eleazara; ndi Eleazara anabala Matani; ndi Matani anabala Yakobo; ndi Yakobo anabala Yosefe, mwamuna wake wa Maria, amene Yesu, wotchedwa Khristu, anabadwa mwa iye. Motero mibadwo yonse kuyambira pa Abrahamu kufikira kwa Davide ndiyo mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa Davide kufikira pa kutengedwa kunka ku Babiloni mibadwo khumi ndi inai; ndi kuyambira pa kutengedwa kunka ku Babiloni kufikira kwa Khristu mibadwo khumi ndi inai. Ndipo kubadwa kwake kwa Yesu Khristu kunali kotere: Amai wake Maria anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanakomane iwowo, anapezedwa iye ali ndi pakati mwa Mzimu Woyera. Koma Yosefe, mwamuna wake, anali wolungama, ndiponso sanafune kunyazitsa iye, nayesa m'mtima kumleka iye m'tseri. Koma pakusinkhasinkha iye zinthu izi, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye m'kulota, nanena, Yosefe, mwana wa Davide, usaope kudzitengera wekha Maria mkazi wako; pakuti icho cholandiridwa mwa iye chili cha Mzimu Woyera. Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake kumachimo ao. Ndipo zonsezi zinakhala kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri, ndi kuti, Onani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, ndipo adzamutcha dzina lake, Imanuele. Ndilo losandulika, Mulungu nafe. Ndipo Yosefe anauka tulo take, nachita monga anamuuza mngelo wa Ambuye, nadzitengera yekha mkazi wake; ndipo sanamdziwe iye kufikira atabala mwana wake; namutcha dzina lake Yesu. Ndipo pa kubadwa kwake kwa Yesu m'Betelehemu wa Yudeya m'masiku a Herode mfumu, onani, Anzeru a kum'mawa anafika ku Yerusalemu, nati, Ali kuti amene anabadwa mfumu ya Ayuda? Chifukwa tinaona nyenyezi yake kum'mawa, ndipo tinadzera kudzamlambira Iye. Ndipo Herode mfumuyo pakumva ichi anavutika, ndi Yerusalemu yense pamodzi naye. Ndipo pamene anasonkhanitsa ansembe aakulu onse ndi alembi a anthu, anafunsira iwo, Adzabadwira kuti Khristuyo? Ndipo anamuuza iye, M'Betelehemu wa Yudeya; chifukwa kunalembedwa kotere ndi mneneri, kuti, Ndipo iwe Betelehemu, dziko la Yudeya, sukhala konse wamng'onong'ono mwa akulu a Yudeya. Pakuti Wotsogolera adzachokera mwa iwe, amene adzaweta anthu anga Aisraele. Pomwepo Herode anawaitana Anzeruwo m'tseri, nafunsitsa iwo nthawi yake idaoneka nyenyeziyo. Nawatumiza ku Betelehemu, nati, Yendani mufunitsitse za kamwanako; ndipo pamene mudzampeza, mundibwezere mau, kuti inenso ndidzadze kudzamlambira Iye. Ndipo iwo, m'mene anamva mfumu, anamuka; ndipo onani, nyenyezi ija anaiona kum'mawa, inawatsogolera iwo, kufikira inadza niima pamwamba pomwe panali kamwanako. Ndipo iwo poona nyenyeziyo, anakondwera ndi kukondwera kwakukulu. Ndipo pofika kunyumba anaona kamwanako ndi Maria amake, ndipo anagwa pansi namgwadira Iye; namasula chuma chao, nampatsa Iye mitulo, ndiyo golide ndi lubani ndi mure. Ndipo iwo, pochenjezedwa m'kulota kuti asabwerere kwa Herode, anachoka kupita ku dziko lao pa njira ina. Ndipo pamene iwo anachoka, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe m'kulota, nati, Tauka, nutenge kamwanako ndi amake, nuthawire ku Ejipito, nukakhale kumeneko kufikira ndidzakuuza iwe; pakuti Herode adzafuna kamwana kukaononga Iko. Ndipo iye ananyamuka natenga kamwana ndi amake usiku, nachoka kupita ku Ejipito; nakhalabe kumeneko kufikira atamwalira Herode; kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri kuti, Ndinaitana Mwana wanga atuluke m'Ejipito. Pamenepo Herode, poona kuti anampusitsa Anzeruwo, anapsa mtima ndithu, natumiza ena kukaononga tiana tonse ta m'Betelehemu ndi ta m'milaga yake yonse, takufikira zaka ziwiri ndi tating'ono tonse, monga mwa nthawi imeneyo iye anafunsitsa kwa Anzeruwo. Pomwepo chinachitidwa chonenedwa ndi Yeremiya mneneri, kuti, Mau anamveka m'Rama, maliro ndi kuchema kwambiri; Rakele wolira ana ake, wosafuna kusangalatsidwa, chifukwa palibe iwo. Koma pakumwalira Herode, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera m'kulota kwa Yosefe m'Ejipito, nati, Tauka, nutenge kamwana ndi amake, nupite kudziko la Israele: chifukwa anafa uja wofuna moyo wake wa kamwanako. Ndipo anauka iye, natenga kamwana ndi amake, nalowa m'dziko la Israele. Koma pakumva iye kuti Arkelao anali mfumu ya Yudeya m'malo mwa atate wake Herode, anachita mantha kupita kumeneko; ndipo pamene anachenjezedwa ndi Mulungu m'kulota, anamuka nalowa kudziko la Galileya, nadza nakhazikika m'mudzi dzina lake Nazarete kuti chikachitidwe chonenedwa ndi aneneri kuti, Adzatchedwa Mnazarayo. Ndipo masiku aja anadza Yohane Mbatizi, nalalikira m'chipululu cha Yudeya, nanena, Tembenukani mitima; chifukwa Ufumu wa Kumwamba wayandikira. Pakuti uyu ndiye ananenayo Yesaya mneneri, kuti, Mau a wofuula m'chipululu, konzani khwalala la Ambuye, lungamitsani njira zake. Ndipo Yohane yekhayo anali nacho chovala chake cha ubweya wangamira, ndi lamba lachikopa m'chuuno mwake; ndi chakudya chake chinali dzombe ndi uchi wa kuthengo. Pamenepo panamtulukira iye a ku Yerusalemu, ndi Yudeya lonse, ndi dziko lonse loyandikana ndi Yordani; nabatizidwa ndi iye mu mtsinjewo wa Yordani, alikuwulula machimo ao. Ndipo iye pakuona ambiri a Afarisi ndi a Asaduki akudza ku ubatizo wake, anati kwa iwo, Obadwa a njoka inu, ndani anakulangizani kuthawa mkwiyo ulinkudza? Onetsani inu zipatso zakuyenera kutembenuka mtima: ndipo musamayesa kunena mwa inu nokha, Atate wathu tili naye Abrahamu; pakuti ndinena kwa inu kuti mwa miyala iyi Mulungu akhoza kuukitsira Abrahamu ana. Ndiponso tsopano lino nkhwangwa yaikidwa pa mizu ya mitengo: chifukwa chake mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino udulidwa nuponyedwa pamoto. Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto: chouluzira chake chili m'dzanja lake, ndipo adzayeretsa padwale pake; ndipo adzasonkhanitsa tirigu wake m'nkhokwe, koma mankhusu adzatentha ndi moto wosazima. Pamenepo Yesu anachokera ku Galileya nadza ku Yordani kwa Yohane, kudzabatizidwa ndi iye. Koma Yohane anati amkanize, nanena, Ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi? Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero. Pamenepo anamlola Iye. Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anatuluka m'madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye; ndipo onani, mau akuchokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera. Pamenepo Yesu anatengedwa ndi Mzimu kunka kuchipululu kukayesedwa ndi mdierekezi. Ndipo pamene Iye analibe kudya masiku makumi anai usana ndi usiku, pambuyo pake anamva njala. Ndipo woyesayo anafika nanena kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, tauzani kuti miyala iyi isanduke mikate. Koma Iye anayankha nati, Kwalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mau onse akutuluka m'kamwa mwa Mulungu. Pamenepo mdierekezi anamuka naye kumzinda woyera; namuika Iye pamwamba penipeni pa Kachisi, nanena naye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, mudzigwetse nokha pansi: pakuti kwalembedwa, kuti, Adzalamula angelo ake za iwe, ndipo pa manja ao adzakunyamula iwe, ungagunde konse phazi lako pamwala. Yesu ananena naye, Ndiponso kwalembedwa, Usamuyese Ambuye Mulungu wako. Pomwepo mdierekezi anamuka naye kuphiri lalitali, namuonetsa maufumu onse a dziko lapansi, ndi ulemerero wao; nati kwa Iye, Zonse ndikupatsani Inu, ngati mudzagwa pansi ndi kundigwadira ine. Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Choka Satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzamgwadira, ndipo Iye yekhayekha udzamlambira. Pomwepo mdierekezi anamsiya Iye, ndipo onani, angelo anadza, namtumikira Iye. Ndipo pamene Yesu anamva kuti anampereka Yohane, anamuka kulowa ku Galileya; ndipo anachoka ku Nazarete nadza nakhalitsa Iye m'Kapernao wa pambali pa nyanja, m'malire a Zebuloni ndi Nafutali: kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Yesaya mneneri, kuti, Dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafutali, njira ya kunyanja, kutsidya lija la Yordani, Galileya la anthu akunja, anthu akukhala mumdima adaona kuwala kwakukulu, ndi kwa iwo okhala m'malo a mthunzi wa imfa, kuwala kunatulukira iwo. Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kulalikira, ndi kunena, Tembenukani mitima, pakuti Ufumu wa Kumwamba wayandikira. Ndipo pamene Yesu analikuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona abale awiri, Simoni wonenedwa Petro, ndi Andrea, mbale wake, analikuponya khoka m'nyanja; popeza anali asodzi a nsomba. Ndipo Iye ananena nao, Tiyeni pambuyo panga, ndidzakusandutsani asodzi a anthu. Ndipo iwo anasiya pomwepo makokawo, namtsata Iye. Ndipo popitirirapo Iye anaona abale ena awiri, Yakobo mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake, m'ngalawa, pamodzi ndi Zebedeo atate wao, analikusoka makoka ao; ndipo anaitana iwo. Ndipo anasiya pomwepo ngalawayo ndi atate wao, namtsata Iye. Ndipo Yesu anayendayenda m'Galileya monse, analikuphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu, nachiritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu. Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa. Ndipo inamtsata mipingomipingo ya anthu ochokera ku Galileya, ndi ku Dekapoli ndi ku Yerusalemu, ndi ku Yudeya, ndi ku tsidya lija la Yordani. Ndipo m'mene Iye anaona makamu, anakwera m'phiri; ndipo m'mene Iye anakhala pansi, anadza kwa Iye ophunzira ake; ndipo anatsegula pakamwa, nawaphunzitsa iwo, nati: Odala ali osauka mumzimu; chifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba. Odala ali achisoni; chifukwa adzasangalatsidwa. Odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi. Odala ali akumva njala ndi ludzu la chilungamo; chifukwa adzakhuta. Odala ali akuchitira chifundo; chifukwa adzalandira chifundo. Odala ali oyera mtima; chifukwa adzaona Mulungu. Odala ali akuchita mtendere; chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu. Odala ali akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo: chifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba. Odala muli inu m'mene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa zilizonse chifukwa cha Ine. Sekerani, sangalalani: chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu m'Mwamba: pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu. Inu ndinu mchere wa dziko lapansi; koma mcherewo ngati ukasukuluka, adzaukoleretsa ndi chiyani? Pamenepo sungakwanirenso kanthu konse, koma kuti ukaponyedwe kunja, nupondedwe ndi anthu. Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mudzi wokhazikika pamwamba pa phiri sungathe kubisika. Kapena sayatsa nyali, ndi kuivundikira m'mbiya, koma aiika iyo pa choikapo chake; ndipo iunikira onse ali m'nyumbamo. Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba. Musaganize kuti ndinadza Ine kudzapasula chilamulo kapena aneneri: sindinadza kupasula, koma kukwaniritsa. Pakuti indetu ndinena kwa inu, Kufikira litapitirira thambo ndi dziko, kalemba kakang'ono kamodzi kapena kansonga kake kamodzi sikadzachokera kuchilamulo, kufikira zitachitidwa zonse. Chifukwa chake yense wakumasula limodzi la malamulo amenewa ang'onong'ono, nadzaphunzitsa anthu chomwecho, adzatchulidwa wamng'onong'ono mu Ufumu wa Kumwamba; koma yense wakuchita ndi kuphunzitsa awa, iyeyu adzatchulidwa wamkulu mu Ufumu wa Kumwamba. Pakuti ndinena ndi inu, ngati chilungamo chanu sichichuluka choposa cha alembi ndi Afarisi, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba. Munamva kuti kunanenedwa kwa iwo akale, Usaphe; koma yense wakupha adzakhala wopalamula mlandu: koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe: adzakhala wopalamula Gehena wamoto. Chifukwa chake ngati ulikupereka mtulo wako pa guwa la nsembe, ndipo pomwepo ukakumbukira kuti mbale wako ali ndi kanthu pa iwe, usiye pomwepo mtulo wako kuguwako, nuchoke, nuyambe kuyanjana ndi mbale wako, ndipo pamenepo idza nupereke mtulo wako. Fulumira kuyanjana ndi mnzako wamlandu, pamene uli naye panjira; kapena mnzako wamlandu angakupereke iwe kwa woweruza mlandu, ndi woweruzayo angapereke iwe kwa msilikali, nuponyedwe iwe m'nyumba yandende. Indetu ndinena ndi iwe, sudzatulukamo konse, koma utalipa kakobiri kakumaliza ndiko. Munamva kuti kunanenedwa, Usachite chigololo; koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang'ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake. Koma ngati diso lako lamanja likulakwitsa iwe, ulikolowole, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe, kuti chimodzi cha ziwalo zako chionongeke, losaponyedwa thupi lako lonse m'Gehena. Ndipo ngati dzanja lako lamanja likulakwitsa iwe, ulidule, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe kuti chimodzi cha ziwalo zako chionongeke, losamuka thupi lako lonse ku Gehena. Kunanenedwanso, Yense wakuchotsa mkazi wake ampatse iye chilekaniro: koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuchotsa mkazi wake, kosati chifukwa cha chigololo, amchititsa chigololo: ndipo amene adzakwata wochotsedwayo achita chigololo. Ndiponso, munamva kuti kunanenedwa kwa iwo akale, Usalumbire konama, koma udzapereka kwa Ambuye zolumbira zako: koma Ine ndinena kwa inu, Musalumbire konse, kapena kutchula Kumwamba, chifukwa kuli chimpando cha Mulungu; kapena kutchula dziko lapansi, chifukwa lili popondapo mapazi ake; kapena kutchula Yerusalemu, chifukwa kuli mzinda wa Mfumu yaikulukulu. Kapena usalumbire kumutu wako, chifukwa sungathe kuliyeretsa mbu kapena kulidetsa bii tsitsi limodzi. Koma manenedwe anu akhale, Inde, inde; Iai, iai; ndipo choonjezedwa pa izo chichokera kwa woipayo. Munamva kuti kunanenedwa, Diso kulipa diso, ndi dzino kulipa dzino: koma ndinena kwa inu, Musakanize munthu woipa; koma amene adzakupanda iwe pa tsaya lako lamanja, umtembenuzire linanso. Ndipo kwa iye wofuna kupita nawe kumlandu ndi kutenga malaya ako, umlolezenso chofunda chako. Ndipo amene akakukakamiza kumperekeza njira imodzi, upite naye ziwiri. Kwa iye wopempha iwe umpatse, ndipo kwa iye wofuna kukukongola usampotolokere. Munamva kuti kunanenedwa, Uzikondana ndi mnansi wako, ndi kumuda mdani wako: koma Ine ndinena kwa inu, Kondanani nao adani anu, ndi kupempherera iwo akuzunza inu; kotero kuti mukakhale ana a Atate wanu wa Kumwamba; chifukwa Iye amakwezera dzuwa lake pa oipa ndi pa abwino, namavumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama. Chifukwa kuti ngati muwakonda akukondana ndi inu mphotho yanji muli nayo? Kodi angakhale amisonkho sachita chomwecho? Ndipo ngati mupatsa moni abale anu okhaokha, muchitanji choposa ena? Kodi angakhale anthu akunja sachita chomwecho? Chifukwa chake inu mukhale angwiro, monga Atate wanu wa Kumwamba ali wangwiro. Yang'anirani kuti musachite zolungama zanu pamaso pa anthu kuti muonekere kwa iwo; pakuti ngati mutero mulibe mphotho ndi Atate wanu wa Kumwamba. Chifukwa chake pamene paliponse upatsa mphatso zachifundo, usamaomba lipenga patsogolo pako, monga amachita onyenga m'masunagoge, ndi m'makwalala, kotero kuti atamandidwe ndi anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao. Koma iwe popatsa mphatso zachifundo, dzanja lako lamanzere lisadziwe chimene lichita dzanja lako lamanja; kotero kuti mphatso zako zachifundo zikhale zam'tseri; ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe. Ndipo pamene mupemphera, musakhale monga onyengawo; chifukwa iwo akonda kuimirira ndi kupemphera m'masunagoge, ndi pa mphambano za makwalala, kuti aonekere kwa anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao. Koma iwe popemphera, lowa m'chipinda chako, nutseke chitseko chako, nupemphere Atate wako ali m'tseri, ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe. Ndipo popemphera musabwerezebwereze chabe iai, monga amachita anthu akunja, chifukwa ayesa kuti adzamvedwa ndi kulankhulalankhula kwao. Chifukwa chake inu musafanane nao: pakuti Atate wanu adziwa zomwe muzisowa, inu musanayambe kupempha Iye. Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano. Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero. Ndipo mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso takhululukira amangawa anthu. Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo. Pakuti ngati mukhululukira anthu zolakwa zao adzakhululukira inunso Atate wanu wa Kumwamba. Koma ngati simukhululukira anthu zolakwa zao, Atate wanunso sadzakhululukira zolakwa zanu. Ndipo pamene ponse musala kudya, musakhale ndi nkhope yachisoni, ngati onyengawo; pakuti aipitsa nkhope zao, kuti aonekere kwa anthu kuti alimkusala kudya. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao. Koma iwe, posala kudya, dzola mutu wako, ndi kusamba nkhope yako: kuti usaonekere kwa anthu kuti ulikusala kudya, koma kwa Atate wako ali m'tseri: ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe. Musadzikundikire nokha chuma pa dziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba: koma mudzikundikire nokha chuma m'Mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba; pakuti kumene kuli chuma chako, komwe udzakhala mtima wakonso. Diso ndilo nyali ya thupi; chifukwa chake ngati diso lako lili la kumodzi, thupi lako lonse lidzakhala lowalitsidwa. Koma ngati diso lako lili loipa, thupi lako lonse lidzakhala lodetsedwa. Chifukwa chake ngati kuwala kumene kuli mwa inu kuli mdima, mdimawo ndi waukulu ndithu! Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma. Chifukwa chake ndinena kwa inu, Musadere nkhawa moyo wanu, chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa; kapena thupi lanu, chimene mudzavala. Kodi moyo suli woposa chakudya, ndi thupi loposa chovala? Yang'anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ai, kapena sizimatutira m'nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi? Ndipo ndani wa inu ndi kudera nkhawa angathe kuonjezera pa msinkhu wake mkono umodzi? Ndipo muderanji nkhawa ndi chovala? Tapenyetsani maluwa a kuthengo, makulidwe ao; sagwiritsa ntchito, kapena sapota: koma ndinena kwa inu, kuti angakhale Solomoni mu ulemerero wake wonse sanavale monga limodzi la amenewa. Koma ngati Mulungu aveka chotero udzu wa kuthengo, ukhala lero, ndi mawa uponyedwa pamoto, nanga si inu kopambana ndithu, inu akukhulupirira pang'ono? Chifukwa chake musadere nkhawa, ndi kuti, Tidzadya chiyani? Kapena, Tidzamwa chiyani? Kapena, Tidzavala chiyani? Pakuti anthu akunja azifunitsa zonse zimenezo; pakuti Atate wanu wa Kumwamba adziwa kuti musowa zonse zimenezo. Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu. Chifukwa chake musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhawa iwo okha. Zikwanire tsiku zovuta zake. Musaweruze, kuti mungaweruzidwe. Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao, kudzayesedwa kwa inunso. Ndipo upenya bwanji kachitsotso kali m'diso la mbale wako, koma mtanda uli m'diso la iwe mwini suuganizira? Kapena udzati bwanji kwa mbale wako, Tandilola ndichotse kachitsotso m'diso lako; ndipo ona, mtandawo ulimo m'diso lakoli. Wonyenga iwe! Tayamba kuchotsa m'diso lako mtandawo, ndipo pomwepo udzapenyetsa kuchotsa kachitsotso m'diso la mbale wako. Musamapatsa chopatulikacho kwa agalu, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi ao, ndi potembenuka zingang'ambe inu. Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu; pakuti yense wakupempha alandira; ndi wakufunayo apeza; ndi kwa wogogodayo chitsegulidwa. Kapena munthu ndani wa inu, amene pompempha mwana wake mkate, adzampatsa mwala? Kapena pompempha nsomba, adzampatsa iye njoka kodi? Chomwecho, ngati inu, muli oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kopambana kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa iwo akumpempha Iye? Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri. Lowani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa icho. Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali owerengeka. Yang'anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma m'kati mwao ali mimbulu yolusa. Mudzawazindikira ndi zipatso zao. Kodi atchera mphesa paminga, kapena nkhuyu pamtula? Chomwecho mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa. Sungathe mtengo wabwino kupatsa zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuchi kupatsa zipatso zokoma. Mtengo uliwonse wosapatsa chipatso chokoma, audula, nautaya kumoto. Inde chomwecho pa zipatso zao mudzawazindikira iwo. Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba. Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera mau m'dzina lanu, ndi m'dzina lanunso kutulutsa ziwanda, ndi kuchita m'dzina lanunso zamphamvu zambiri? Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziwani inu nthawi zonse; chokani kwa Ine, inu akuchita kusaweruzika. Chifukwa chimenechi yense amene akamva mau anga amenewa, ndi kuwachita, ndidzamfanizira iye ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe; ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; koma siinagwa; chifukwa inakhazikika pathanthwepo. Ndipo yense akamva mau anga amenewa, ndi kusawachita, adzafanizidwa ndi munthu wopusa, yemwe anamanga nyumba yake pamchenga; ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; ndipo inagwa; ndi kugwa kwake kunali kwakukulu. Ndipo panakhala pamene Yesu anatha mau amenewa, makamu a anthu anazizwa ndi chiphunzitso chake: pakuti anawaphunzitsa monga mwini mphamvu, wosanga alembi ao. Ndipo pakutsika pake paphiripo, inamtsata mipingo yambiri ya anthu. Ndipo onani, wakhate anadza namgwadira Iye, nanena, Ambuye ngati mufuna mungathe kundikonza. Ndipo Yesu anatambalitsa dzanja lake, namkhudza iye, nati, Ndifuna; takonzedwa. Ndipo pomwepo khate lake linachoka. Ndipo Yesu ananena naye, Ona, iwe, usauze munthu; koma muka, udzionetse wekha kwa wansembe, nupereke mtulo umene anaulamulira Mose, ukhale mboni kwa iwo. Ndipo m'mene Iye analowa m'Kapernao anadza kwa Iye kenturiyo, nampemba Iye, nati, Ambuye, mnyamata wanga ali gone m'nyumba wodwala manjenje, wozunzidwa koopsa. Ndipo Yesu ananena naye, Ndifika Ine, ndidzamchiritsa iye. Koma kenturiyoyo anavomera nati, Ambuye, sindiyenera kuti mukalowe pansi pa chindwi langa iai; koma mungonena mau, ndipo adzachiritsidwa mnyamata wanga. Pakuti inenso ndili munthu wakumvera ulamuliro, ndili nao asilikali akundimvera ine: ndipo ndinena kwa uyu, Muka, namuka; ndi kwa wina, Idza, nadza; ndi kwa kapolo wanga, Chita ichi, nachita. Ndipo pakumva ichi, Yesu anazizwa, nati kwa iwo akumtsata, Indetu ndinena kwa inu, ngakhale mwa Israele, sindinapeza chikhulupiriro chotere. Ndipo ndinena ndi inu, kuti ambiri a kum'mawa ndi a kumadzulo adzafika, nadzakhala pamodzi ndi Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, mu Ufumu wa Kumwamba; koma anawo a Ufumu adzatayidwa kumdima wakunja; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano. Ndipo Yesu anati kwa kenturiyoyo, Pita, kukhale kwa iwe monga unakhulupirira. Ndipo anachiritsidwa mnyamatayo nthawi yomweyo. Ndipo pofika Yesu kunyumba ya Petro, anaona mpongozi wake ali gone, alikudwala malungo. Ndipo anamkhudza dzanja lake, ndipo malungo anamleka mkaziyo; ndipo anauka, namtumikira Iye. Ndipo pakudza madzulo, anabwera nao kwa Iye anthu ambiri ogwidwa ndi ziwanda; ndipo Iye anatulutsa mizimuyo ndi mau, nachiritsa akudwala onse; kotero kuti chikwaniridwe chonenedwa ndi Yesaya mneneri, kuti, Iye yekha anatenga zofooka zathu, nanyamula nthenda zathu. Ndipo Yesu, poona makamu ambiri a anthu akumzungulira Iye, analamulira ophunzira amuke kutsidya lina. Ndipo anadza munthu mlembi, nati kwa Iye, Mphunzitsi, ndidzakutsatani Inu kulikonse mumukako. Ndipo Yesu ananena kwa iye, Ankhandwe ali nazo nkhwimba zao, ndi mbalame za m'mlengalenga zisa zao, koma Mwana wa Munthu alibe potsamira mutu wake. Ndipo wina wa ophunzira ake anati kwa Iye, Ambuye, mundilole ine nditange ndamuka kuika maliro a atate wanga. Koma Yesu ananena kwa iye, Tsata Ine, nuleke akufa aike akufa ao. Ndipo pamene Iye atalowa m'ngalawa, ophunzira ake anamtsata Iye. Ndipo onani, panauka namondwe wamkulu panyanja, kotero kuti ngalawa inafundidwa ndi mafunde: koma Iye anali m'tulo. Ndipo iwo anadza, namuutsa Iye, nanena, Ambuye, tipulumutseni, tilikutayika. Ndipo ananena Iye kwa iwo, Muli amantha bwanji, okhulupirira pang'ono inu? Pomwepo Iye anauka, nadzudzula mphepo ndi nyanja, ndipo panagwa bata lalikulu. Ndipo anazizwa anthuwo nanena, Ndiye munthu wotani uyu, pakuti ngakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye? Ndipo pofika Iye kutsidya lina, kudziko la Agadara, anakomana naye awiri ogwidwa ndi ziwanda, akutuluka kumanda, aukali ndithu, kotero kuti sangathe kupitapo munthu pa njira imeneyo. Ndipo onani, anafuula nati, Tili nanu chiyani, Inu Mwana wa Mulungu? Mwadza kuno kodi kutizunza ife, nthawi yake siinafike? Ndipo panali patali ndi iwo gulu la nkhumba zambiri zilinkudya. Ndipo mizimuyo inampempha Iye ninena, Ngati mutitulutsa, mutitumize ife tilowe m'gulu la nkhumbazo. Ndipo anati kwa iyo, Mukani. Ndipo inatuluka, nimuka, kukalowa m'nkhumbazo; ndipo onani, gulu lonse linathamangira kunsi kuphompho m'nyanjamo, ndipo linafa m'madzi. Koma akuziweta anathawa, namuka kumidzi, nauza zonse, ndi zakuti zao za aziwanda aja. Ndipo onani, mudzi wonse unatulukira kukakumana naye Yesu, ndipo m'mene anamuona Iye, anampempha kuti achoke m'malire ao. Ndipo Iye analowa m'ngalawa, naoloka, nadza kumudzi kwao. Ndipo onani, anabwera naye kwa Iye munthu wamanjenje, wakugona pamphasa: ndipo Yesu pakuona chikhulupiriro chao, anati kwa wodwalayo, Limba mtima, mwana, machimo ako akhululukidwa. Ndipo onani, ena a alembi ananena mumtima mwao, Uyu achitira Mulungu mwano. Ndipo Yesu, pozindikira maganizo ao, anati, Chifukwa chanji mulinkuganizira zoipa m'mitima yanu? Pakuti chapafupi nchiti, kunena, Machimo ako akhululukidwa; kapena kunena, Tanyamuka. Nuyende? Koma kuti mudziwe kuti ali nazo mphamvu Mwana wa Munthu pansi pano za kukhululukira machimo (pomwepo ananena kwa wodwalayo), Tanyamuka, nutenge mphasa yako, numuke kunyumba kwako. Ndipo ananyamuka, napita kunyumba kwake. Ndipo m'mene anthu a makamu anachiona, anaopa, nalemekeza Mulungu, wakupatsa anthu mphamvu yotere. Ndipo Yesu popita, kuchokera kumeneko, anaona munthu, dzina lake Mateyu, alinkukhala polandirira msonkho, nanena kwa iye, Nditsate Ine. Ndipo iye anauka, namtsata. Ndipo panali pamene Iye analinkukhala pachakudya m'nyumba, onani, amisonkho ndi ochimwa ambiri anadza nakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake. Ndipo Afarisi, pakuona ichi, ananena kwa ophunzira ake, Chifukwa ninji Mphunzitsi wanu alinkudya pamodzi ndi amisonkho ndi ochimwa? Ndipo m'mene Yesu anamva anati, Olimba safuna sing'anga ai, koma odwala. Koma mukani muphunzire nchiyani ichi, Ndifuna chifundo, si nsembe ai; pakuti sindinadza kudzaitana olungama, koma ochimwa. Pomwepo anadza kwa Iye ophunzira ake a Yohane, nati, Chifukwa ninji ife ndi Afarisi tisala kudya kawirikawiri, koma ophunzira anu sasala? Ndipo Yesu anati kwa iwo, Nanga anyamata a nyumba ya ukwati angathe kulira kodi nthawi imene mkwati akhala nao? Koma adzafika masiku, pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo pomwepo adzasala kudya. Ndipo kulibe munthu aphathika chigamba cha nsalu yaiwisi pa chofunda chakale; pakuti chigamba chake chizomoka kuchofundacho, ndipo chichita chiboo chachikulu. Kapena samathira vinyo watsopano m'matumba akale; akatero, matumba aphulika, ndi vinyo atayika, ndi matumba aonongeka; koma athira vinyo watsopano m'matumba atsopano, ndi zonse ziwiri zisungika. M'mene Iye analikulankhula nao zinthu zimenezo, onani, anadza munthu mkulu, namgwadira Iye, nanena, Wamwalira tsopanoli mwana wanga wamkazi, komatu mudze muike dzanja lanu pa iye, ndipo adzakhala ndi moyo. Ndipo Yesu ananyamuka namtsata iye, ndi ophunzira ake omwe. Ndipo onani, mkazi, anali ndi nthenda yachidwalire zaka khumi ndi ziwiri, anadza pambuyo pake, nakhudza mphonje ya chofunda chake; pakuti analikunena mwa iye yekha, Ngati ndingakhudze chofunda chake chokha ndidzachira. Koma Yesu potembenuka ndi kuona iye anati, Limba mtima, mwana wamkaziwe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Ndipo mkaziyo anachira kuyambira nthawi yomweyo. Ndipo Yesu polowa m'nyumba yake ya mkuluyo, ndi poona oimba zitoliro ndi khamu la anthu obuma, ananena, Tulukani, pakuti kabuthuko sikanafa koma kali m'tulo. Ndipo anamseka Iye pwepwete. Koma pamene khamulo linatulutsidwa, Iye analowamo, nagwira dzanja lake; ndipo kabuthuko kadauka. Ndipo mbiri yake imene inabuka m'dziko lonse limenelo. Ndipo popita Yesu kuchokera kumeneko, anamtsata Iye anthu awiri akhungu, ofuula ndi kuti, Mutichitire ife chifundo, mwana wa Davide. Ndipo m'mene Iye analowa m'nyumbamo, akhunguwo anadza kwa Iye; ndipo Yesu anati kwa iwo, Mukhulupirira kodi kuti ndikhoza kuchita ichi? Anena kwa Iye, Inde, Ambuye. Pomwepo anakhudza maso ao, nati, Chichitidwe kwa inu monga chikhulupiriro chanu. Ndipo maso ao anaphenyuka. Ndipo Yesu anawauzitsa iwo, nanena, Yang'anirani, asadziwe munthu aliyense. Koma iwo anatulukamo, nabukitsa mbiri yake m'dziko lonselo. Ndipo pamene iwo analikutuluka, onani, anabwera naye kwa Iye munthu wosalankhula, wogwidwa ndi chiwanda. Ndipo m'mene chinatulutsidwa chiwandacho, wosalankhulayo analankhula, ndipo makamu a anthu anazizwa, nanena, Kale lonse sichinaoneke chomwecho mwa Israele. Koma Afarisi analinkunena, Atulutsa ziwanda ndi mphamvu zake za mfumu ya ziwanda. Ndipo Yesu anayendayenda m'mizinda yonse ndi m'midzi, namaphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumuwo, nachiritsa nthenda iliyonse ndi zofooka zonse. Koma Iye, poona makamuwo, anagwidwa m'mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa. Pomwepo ananena kwa ophunzira ake, Zotuta zichulukadi koma antchito ali owerengeka. Chifukwa chake pempherani Mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake. Ndipo pamene Iye anadziitanira ophunzira ake khumi ndi awiri, anapatsa iwo mphamvu pa mizimu yoipa, yakuitulutsa, ndi yakuchiza nthenda iliyonse ndi zofooka zonse. Ndipo maina ao a atumwiwo khumi ndi awiri ndi awa: woyamba Simoni wotchedwa Petro, ndi Andrea mbale wake; Yakobo mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake; Filipo, ndi Bartolomeo; Tomasi, ndi Mateyu wamsonkhoyo; Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo; Simoni Mkanani, ndi Yudasi Iskariote amenenso anampereka Iye. Awa amene, khumi ndi awiriwa, Yesu anawatumiza, nawalangiza ndi kuti, Musapite kunjira ya kwa anthu akunja, ndi m'mudzi wa Asamariya musamalowamo: koma makamaka mupite kunkhosa zosokera za banja la Israele. Ndipo pamene mulikupita lalikani kuti, Ufumu wa Kumwamba wayandikira. Chiritsani akudwala, ukitsani akufa, konzani akhate, tulutsani ziwanda: munalandira kwaulere, patsani kwaulere. Musadzitengere ndalama zagolide, kapena zasiliva, kapena zakobiri m'malamba mwanu; kapena thumba la kamba la kunjira, kapena malaya awiri, kapena nsapato, kapena ndodo; pakuti wantchito ayenera kulandira zakudya zake. Ndipo m'mzinda uliwonse, kapena m'mudzi. Mukalowamo, mufunsitse amene ali woyenera momwemo; ndipo bakhalani komweko kufikira mutulukamo. Ndipo polowa m'nyumba muwalonjere. Ndipo ngati nyumbayo ili yoyenera, mtendere wanu udze pa iyo, koma ngati siili yoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu. Ndipo yemwe sadzakulandirani inu kapena kusamva mau anu, pamene mulikutuluka m'nyumbayo, kapena m'mudzimo, sansani fumbi m'mapazi anu. Indetu ndinena kwa inu, kuti, tsiku la kuweruza, mlandu wao wa Sodomu ndi Gomora udzachepa ndi wake wa mudzi umenewo. Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda. Koma chenjerani ndi anthu; pakuti adzakuperekani inu kwa akulu a mlandu, nadzakukwapulani inu m'masunagoge mwao; ndiponso adzamuka nanu kwa akazembe ndi mafumu chifukwa cha Ine, kukhala mboni ya kwa iwo, ndi kwa anthu akunja. Koma pamene paliponse angakuperekeni inu, musamadera nkhawa mudzalankhule bwanji kapena mudzanene chiyani; pakuti chimene mudzachilankhula, chidzapatsidwa kwa inu nthawi yomweyo; pakuti wolankhula si ndinu, koma Mzimu wa Atate wanu akulankhula mwa inu. Ndipo mbale adzapereka mbale wake kuimfa, ndi atate mwana wake: ndipo ana adzatsutsa akuwabala, nadzawafetsa iwo. Ndipo adzada inu anthu onse chifukwa cha dzina langa; koma iye wakupirira kufikira chimaliziro, iyeyu adzapulumutsidwa. Koma pamene angakuzunzeni inu m'mudzi uwu, thawirani mwina: indetu ndinena kwa inu, Simudzaitha mizinda ya Israele, kufikira Mwana wa Munthu atadza. Wophunzira saposa mphunzitsi wake, kapena kapolo saposa mbuye wake. Kumkwanira wophunzira kuti akhale monga mphunzitsi wake, ndi kapolo monga mbuye. Ngati anamutcha mwini banja Belezebulu, sadzaposa kodi kuwatero apabanja ake? Chifukwa chake musaopa iwo; pakuti palibe kanthu kanavundikiridwa, kamene sikadzaululidwa; kapena kanthu kobisika, kamene sikadzadziwika. Chimene ndikuuzani inu mumdima, tachinenani poyera; ndi chimene muchimva m'khutu, muchilalikire pa machindwi a nyumba. Ndipo musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muope Iye, wokhoza kuononga moyo ndi thupi lomwe m'Gehena. Kodi mpheta ziwiri sizigulidwa kakobiri? Ndipo imodzi ya izo siigwa pansi popanda Atate wanu: komatu inu, matsitsi onse a m'mutu mwanu awerengedwa. Chifukwa chake musamaopa; inu mupambana mpheta zambiri. Chifukwa chake yense amene adzavomereza Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzamvomereza iye pamaso pa Atate wanga wa Kumwamba. Koma yense amene adzandikana Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzamkana iye pamaso pa Atate wanga wa Kumwamba. Musalingalire kuti ndidadzera kuponya mtendere pa dziko lapansi; sindinadzera kuponya mtendere, koma lupanga. Pakuti ndinadza kusiyanitsa munthu ndi atate wake, ndi mwana wamkazi ndi amake, ndi mkazi wokwatiwa ndi mpongozi wake: ndipo apabanja ake a munthu adzakhala adani ake. Iye wakukonda atate wake, kapena amake koposa Ine, sayenera Ine, ndipo iye wakukonda mwana wake wamwamuna, kapena wamkazi koposa Ine, sayenera Ine. Ndipo iye amene satenga mtanda wake, natsata pambuyo panga, sayenera Ine. Iye amene apeza moyo wake, adzautaya; ndi iye amene ataya moyo wake, chifukwa cha Ine, adzaupeza. Iye wakulandira inu, andilandira Ine, ndi wakundilandira Ine, amlandira Iye amene ananditumiza Ine. Iye wakulandira mneneri, pa dzina la mneneri, adzalandira mphotho ya mneneri; ndipo wakulandira munthu wolungama, pa dzina la munthu wolungama adzalandira mphotho ya munthu wolungama. Ndipo amene aliyense adzamwetsa mmodzi wa ang'ono awa chikho chokha cha madzi ozizira, pa dzina la wophunzira, indetu ndinena kwa inu, iye sadzataya mphotho yake. Ndipo panali, pamene Yesu anatha kuwafotokozera ophunzira ake khumi ndi awiri, Iye anachokera kumeneko kukaphunzitsa ndi kulalikira m'midzi mwao. Koma Yohane, pakumva m'nyumba yandende ntchito za Khristu, anatumiza ophunzira ake mau, nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina? Ndipo Yesu anayankha, nanena nao, Mukani mubwezere mau kwa Yohane zimene muzimva ndi kuziona: akhungu alandira kuona kwao, ndi opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ndi ogontha akumva, ndi akufa aukitsidwa, ndi kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino. Ndipo wodala iye amene sakhumudwa chifukwa cha Ine. Ndipo m'mene iwo analikumuka, Yesu anayambonena ndi makamu a anthu za kwa Yohane, Munatuluka kunka kuchipululu kukapenya nji? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi? Koma munatuluka kukaona chiyani? Munthu wovala zofewa kodi? Onani, akuvala zofewa ali m'nyumba zamafumu. Koma munatulukiranji? Kukaona mneneri kodi? Indetu, ndinena kwa inu, wakuposa mneneri. Uyu ndiye amene kunalembedwa za iye, kuti, Onani Ine nditumiza mthenga wanga pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu m'tsogolo mwanu. Indetu ndinena kwa inu, Sanauke wakubadwa mwa mkazi munthu wamkulu woposa Yohane Mbatizi; koma iye amene ali wochepa mu Ufumu wa Kumwamba amkulira iye. Ndipo kuyambira masiku a Yohane Mbatizi, kufikira tsopano lino, Ufumu wa Kumwamba uli wokakamizidwa, ndipo okakamirawo aukwatula ndi mphamvu. Pakuti aneneri onse ndi chilamulo chinanenera kufikira pa Yohane. Ndipo ngati mufuna kulandira, uyu ndiye Eliya amene amati akudza. Amene ali ndi makutu akumva, amve. Koma ndidzafanizira ndi chiyani obadwa awa a makono? Ali ofanana ndi ana akukhala m'mabwalo a malonda, amene alikuitana anzao. Ndi kuti, Tinakulizirani inu zitoliro, ndipo inu simunavina; tinabuma maliro, ndipo inu simunalira. Pakuti Yohane anadza wosadya, wosamwa, ndipo iwo amati, Ali ndi chiwanda. Mwana wa Munthu anadza wakudya, ndi wakumwa, ndipo iwo amati, Onani munthu wakudyaidya ndi wakumwaimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi ochimwa! Ndipo nzeru iyesedwa yolungama ndi ntchito zake. Pomwepo Iye anayamba kutonza midziyo, m'mene zinachitidwa zambiri za ntchito zamphamvu zake, chifukwa kuti siinatembenuke. Tsoka kwa iwe, Korazini! Tsoka kwa iwe, Betsaida! Chifukwa ngati zamphamvu zimene zachitidwa mwa inu zikadachitidwa m'Tiro ndi m'Sidoni, akadatembenuka mtima kalekale m'ziguduli ndi m'phulusa. Komanso ndinena kwa inu kuti tsiku la kuweruza mlandu wao wa Tiro ndi Sidoni udzachepa ndi wanu. Ndipo iwe, Kapernao, udzakwezedwa kodi kufikira kuthambo? Udzatsika kufikira ku dziko la akufa! Chifukwa ngati zamphamvu zimene zachitidwa mwa iwe zikadachitidwa m'Sodomu, uyo ukadakhala kufikira lero. Komanso ndinena kwa inu kuti tsiku la kuweruza, mlandu wake wa Sodomu udzachepa ndi wako. Nyengo imeneyo Yesu anayankha nati, Ndivomerezana ndi Inu, Atate, Mwini Kumwamba ndi dziko lapansi, kuti munazibisira izo kwa anzeru ndi akudziwitsa, ndipo munaziululira zomwe kwa makanda: etu, Atate, chifukwa chotero chinakhala chokondweretsa pamaso panu. Zinthu zonse zinaperekedwa kwa Ine ndi Atate wanga; ndipo palibe munthu adziwa Mwana yekha, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira. Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka. Nyengo imeneyo Yesu anapita tsiku la Sabata pakati pa minda ya tirigu; ndipo ophunzira ake anali ndi njala, nayamba kubudula ngala, nadya. Koma Afarisi, pakuona, anati kwa Iye, Tapenyani, ophunzira anu achita chosaloleka tsiku la Sabata. Koma Iye anati kwa iwo, Kodi simunawerenga chimene anachichita Davide, pamene anali ndi njala, ndi iwo amene anali naye? Kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, nadya mikate yoonetsa, imene yosaloleka kudya iye kapena amene anali naye, koma ansembe okhaokha. Kapena simunawerenga kodi m'chilamulo, kuti tsiku la Sabata ansembe m'Kachisi amaipitsa tsiku la Sabata, nakhala opanda tchimo? Koma ndinena kwa inu, kuti wakuposa Kachisiyo ali pompano. Koma mukadadziwa nchiyani ichi, Ndifuna chifundo, si nsembe ai; simukadaweruza olakwa iwo osachimwa, pakuti Mwana wa Munthu ali mwini tsiku la Sabata. Ndipo Iye anachokera pamenepo, nalowa m'sunagoge mwao; ndipo onani, munali munthu wa dzanja lopuwala. Ndipo anamfunsitsa Iye, ndi kuti, Nkuloleka kodi kuchiritsa tsiku la Sabata? Kuti ampalamulitse mlandu. Koma Iye anati kwa iwo, Munthu ndani wa inu, amene ali nayo nkhosa imodzi, ndipo ngati idzagwa m'dzenje tsiku la Sabata, kodi sadzaigwira, ndi kuitulutsa? Nanga kuposa kwake kwa munthu ndi nkhosa nkotani! Chifukwa cha ichi nkuloleka kuchita zabwino tsiku la Sabata. Pomwepo ananena Iye kwa munthuyo, Tansa dzanja lako. Ndipo iye analitansa, ndipo linabwezedwa lamoyo longa linzake. Ndipo Afarisi anatuluka, nakhala upo womchitira Iye mwa kumuononga. Koma Yesu m'mene anadziwa, anachokera kumeneko: ndipo anamtsata Iye anthu ambiri; ndipo Iye anawachiritsa iwo onse, nawalimbitsira mau kuti asamuwulule Iye; kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Yesaya mneneri uja, kuti, Taona mnyamata wanga, amene ndinamsankha, wokondedwa wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; pa Iye ndidzaika Mzimu wanga, ndipo Iye adzalalikira chiweruzo kwa akunja. Sadzalimbana, sadzafuula; ngakhale mmodzi sadzamva mau ake m'makwalala; bango lophwanyika sadzalithyola, ndi nyali yofuka sadzaizima, kufikira Iye adzatumiza chiweruzo chikagonjetse. Ndipo akunja adzakhulupirira dzina lake. Pomwepo anabwera naye kwa Iye munthu wogwidwa ndi chiwanda, wakhungu ndi wosalankhula; ndipo Iye anamchiritsa, kotero kuti wosalankhulayo analankhula, napenya. Ndipo makamu onse a anthu anazizwa, nanena, Uyu si mwana wa Davide kodi? Koma Afarisi pakumva, anati, Uyu samatulutsa ziwanda koma ndi mphamvu yake ya Belezebulu, mkulu wa ziwanda. Ndipo Yesu anadziwa maganizo ao, nati kwa iwo, Ufumu uliwonse wogawanika pa wokha sukhalira kupasuka, ndi mudzi uliwonse kapena banja logawanika pa lokha silidzakhala; ndipo ngati Satana amatulutsa Satana, iye agawanika pa yekha; ndipo udzakhala bwanji ufumu wake? Ndipo ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu yake ya Belezebulu, ana anu amazitulutsa ndi mphamvu ya yani? Chifukwa chake iwo adzakhala oweruza anu. Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu yake ya Mzimu wa Mulungu, pomwepo Ufumu wa Mulungu unafika pa inu. Kapena akhoza bwanji munthu kulowa m'banja la munthu wolimba, ndi kufunkha akatundu ake, ngati iye sayamba kumanga munthu wolimbayo? Ndipo pamenepo adzafunkha za m'banja lake. Iye wosakhala pamodzi ndi Ine akana Ine, ndi iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwazamwaza. Chifukwa chake ndinena kwa inu, Machimo onse, ndi zonena zonse zamwano, zidzakhululukidwa kwa anthu; koma chamwano cha pa Mzimu Woyera sichidzakhululukidwa. Ndipo amene aliyense anganenere Mwana wa Munthu zoipa, adzakhululukidwa; koma amene aliyense anganenere Mzimu Woyera zoipa sadzakhululukidwa nthawi yino kapena ilinkudzayo. Ukakoma mtengo, chipatso chake chomwe chikoma; ukaipa mtengo, chipatso chake mtengo udziwika. Akubadwa inu a njoka, mungathe bwanji kulankhula zabwino, inu akukhala oipa? Pakuti m'kamwa mungolankhula mwa kusefuka kwake kwa mtima. Munthu wabwino atulutsa zabwino m'chuma chake chabwino, ndi munthu woipa atulutsa zoipa m'chuma chake choipa. Ndipo ndinena kwa inu, kuti mau onse opanda pake, amene anthu adzalankhula, adzawawerengera mlandu wake tsiku la kuweruza. Pakuti udzayesedwa wolungama ndi mau ako, ndipo ndi mau ako omwe udzatsutsidwa. Pomwepo alembi ndi Afarisi ena anayankha Iye nati, Mphunzitsi, tifuna kuona chizindikiro cha Inu. Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Akubadwa oipa achigololo afunafuna chizindikiro; ndipo sichidzapatsidwa kwa iwo chizindikiro, komatu chizindikiro cha Yona mneneri; pakuti monga Yona anali m'mimba mwa chinsomba masiku atatu ndi usiku wake, chomwecho Mwana wa Munthu adzakhala mumtima mwa dziko lapansi masiku atatu ndi usiku wake. Anthu a ku Ninive adzauka pamlandu pamodzi ndi obadwa amakono, nadzawatsutsa; chifukwa iwo anatembenuka mtima ndi kulalikira kwake kwa Yona; ndipo onani, wakuposa Yona ali pano. Mfumu yaikazi ya kumwera adzauka pamlandu pamodzi ndi obadwa amakono, nadzawatsutsa; chifukwa iye anachokera kumathero a dziko lapansi kudzamva nzeru ya Solomoni; ndipo onani, wakuposa Solomoni ali pano. Koma mzimu wonyansa, utatuluka mwa munthu, umapitirira malo opanda madzi kufunafuna mpumulo, osaupeza. Pomwepo unena, Ndidzabwerera kunka kunyumba kwanga, konkuja ndinatulukako; ndipo pakufikako uipeza yopanda wokhalamo, yosesedwa ndi yokonzedwa. Pomwepo upita, nutenga pamodzi ndi uwu mizimu ina inzake isanu ndi iwiri yoipa yoposa mwini yekhayo, ndipo ilowa, nikhalamo. Ndipo matsirizidwe ake a munthu uyo akhala oipa oposa mayambidwe ake. Kotero kudzakhalanso kwa obadwa oipa amakono. Pamene Iye anali chilankhulire ndi makamu, onani, amake ndi abale ake anaima panja, nafuna kulankhula naye. Ndipo munthu anati kwa Iye, Onani, amai wanu ndi abale anu aima pabwalo, nafuna kulankhula nanu. Koma Iye anayankha, nati kwa iye wonenayo, Amai wanga ndani, ndipo abale anga ndi ayani? Ndipo anatambalitsa dzanja lake pa ophunzira ake, nati, Penyani amai wanga ndi abale anga! Pakuti aliyense amene adzachita chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo wanga, ndi amai wanga. Tsiku lomwelo Yesu anatuluka m'nyumbamo, nakhala pansi m'mbali mwa nyanja. Ndipo makamu ambiri a anthu anasonkhanira kwa Iye, kotero kuti Iye analowa m'ngalawa, nakhala pansi, ndipo khamu lonse linaima pamtunda. Ndipo Iye anawauzira zinthu zambiri m'mafanizo, nanena, Onani, wofesa anatuluka kukafesa mbeu. Ndipo m'kufesa kwake zina zinagwa m'mbali mwa njira, ndipo zinadza mbalame, nizilusira izo. Koma zina zinagwa pamiyala, pamene panalibe dothi lambiri; ndipo pomwepo zinamera, pakuti sizinakhala nalo dothi lakuya. Ndipo m'mene dzuwa linakwera zinapserera; ndipo popeza zinalibe mizu zinafota. Koma zina zinagwa paminga, ndipo mingayo inayanga, nizitsamwitsa izo. Koma zina zinagwa pa nthaka yabwino, ndipo zinabala zipatso, zina za makumi khumi, zina za makumi asanu ndi limodzi, zina za makumi atatu. Amene ali ndi makutu, amve. Ndipo ophunzirawo anadza, nati kwa Iye, Chifukwa chanji muphiphiritsira iwo m'mafanizo? Ndipo Iye anayankha nati, Chifukwa kwapatsidwa kwa inu kudziwa zinsinsi za Ufumu wa Kumwamba, koma sikunapatsidwa kwa iwo. Pakuti yense amene ali nazo, kudzapatsidwa kwa iye, ndimo adzakhala nazo zochuluka; koma yense amene alibe, chingakhale chomwe ali nacho chidzachotsedwa kwa iye. Chifukwa chake ndiphiphiritsira iwo m'mafanizo; chifukwa kuti akuona samaona, ndi akumva samamva, kapena samadziwitsa. Ndipo adzachitidwa kwa iwo mau adanenera Yesaya, amene ati, Pakumva mudzamva, ndipo simudzazindikira konse; pakupenya mudzapenya, ndipo simudzaona konse. Chifukwa unalemera mtima wa anthu awa, ndipo m'makutu ao anamva mogontha, ndipo maso ao anatsinzina; kuti asaone konse ndi maso, asamve ndi makutu, asazindikire ndi mtima wao, asatembenuke, ndipo ndisawachiritse iwo. Koma maso anu ali odala, chifukwa apenya; ndi makutu anu chifukwa amva. Pakuti indetu ndinena kwa inu, kuti aneneri ambiri ndi anthu olungama analakalaka kupenya zimene muzona, koma sanazione; ndi kumva zimene muzimva, koma sanazimve. Ndipo tsono mverani inu fanizolo la wofesa mbeu uja. Munthu aliyense wakumva mau a Ufumu, osawadziwitsai, woipayo angodza, nakwatula chofesedwacho mumtima mwake. Uyo ndiye wofesedwa m'mbali mwa njira. Koma iye amene afesedwa pamiyala, uyu ndiye wakumva mau, ndi kuwalandira pomwepo ndi kusekera; ndipo alibe mizu mwa iye, koma akhala nthawi yaing'ono; ndipo pakudza nsautso kapena zunzo chifukwa cha mau, iye akhumudwa pomwepo. Ndipo iye amene afesedwa kuminga, uyu ndiye wakumva mau; ndipo kulabadira kwa dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma chitsamwitsa mau, ndipo akhala wopanda chipatso. Ndipo iye amene afesedwa pa nthaka yabwino, uyu ndiye wakumva mau nawadziwitsa; amene abaladi zipatso, nazifitsa, ena za makumi khumi, ena za makumi asanu ndi limodzi, ena za makumi atatu. Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu, amene anafesa mbeu zabwino m'munda mwake; koma m'mene anthu analinkugona, mdani wake anadza, nafesa namsongole pakati pa tirigu, nachokapo. Koma pamene mmera unakula, nubala chipatso, pomwepo anaonekeranso namsongole. Ndipo anyamata ake a mwini nyumbayo anadza, nati kwa iye, Mbuye, kodi simunafesa mbeu zabwino m'munda mwanu? Nanga wachokera kuti namsongoleyo? Ndipo iye ananena kwa iwo, Munthu mdani wanga wachichita ichi. Ndipo anyamata anati kwa iye, Kodi mufuna tsopano kuti timuke, tikamsonkhanitse uyo pamodzi? Koma iye anati, Iai, kuti kapena m'mene mukasonkhanitsa namsongoleyo, mungazulenso tirigu pamodzi naye. Kazilekeni zonse ziwiri, zikulire pamodzi kufikira pakututa; ndimo m'nyengo yakututa ndidzauza akututawo, Muyambe kusonkhanitsa namsongole, mummange uyu mitolo kukamtentha, koma musonkhanitse tirigu m'nkhokwe yanga. Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana ndi kambeu kampiru, kamene anakatenga munthu, nakafesa pamunda pake; kamene kakhaladi kakang'ono koposa mbeu zonse, koma katakula, kali kakakulu kuposa zitsamba zonse, nukhala mtengo, kotero kuti mbalame za mlengalenga zimadza, nizibindikira mu nthambi zake. Fanizo lina ananena kwa iwo; Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana ndi chotupitsa mikate, chimene mkazi anachitenga, nachibisa m'miyeso itatu ya ufa, kufikira wonse unatupa. Zonsezi Yesu anaziphiphiritsira m'mafanizo kwa makamu a anthu; ndipo kopanda fanizo sanalankhule kanthu kwa iwo; kuti chikachitidwe chonenedwa ndi mneneri, kuti, Ndidzatsegula pakamwa panga ndi mafanizo; ndidzawulula zinthu zobisika chiyambire kukhazikidwa kwake kwa dziko lapansi. Pomwepo Iye anasiya makamuwo, nalowa m'nyumba; ndimo ophunzira ake anadza kwa Iye, nanena, Mutitanthauzire fanizo lija la namsongole wa m'munda. Ndipo Iye anayankha nati, Wofesa mbeu yabwino ndiye Mwana wa Munthu; Ndipo munda ndiwo dziko lapansi; ndi mbeu yabwino ndiyo ana a Ufumuwo; ndi namsongole ndiye ana a woipayo; ndipo mdani amene anamfesa uwu, ndiye mdierekezi: ndi kututa ndicho chimaliziro cha nthawi ya pansi pano; ndi otutawo ndiwo angelo. Ndipo monga namsongole asonkhanitsidwa pamodzi, natenthedwa pamoto, motero mudzakhala m'chimaliziro cha nthawi ya pansi pano. Mwana wa Munthu adzatuma angelo ake, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi, ndi kuchotsa mu Ufumu wake zokhumudwitsa zonse, ndi anthu akuchita kusaweruzika, ndipo adzawataya iwo m'ng'anjo yamoto; kumeneko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano. Pomwepo olungamawo adzawalitsa monga dzuwa, mu Ufumu wa Atate wao. Amene ali ndi makutu amve. Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi chuma chobisika m'munda; chimene munthu anachipeza, nachibisa; ndipo m'kuchikonda kwake achoka, nagulitsa zonse ali nazo, nagula munda umenewu. Ndiponso Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi munthu wa malonda, wakufuna ngale zabwino: ndipo m'mene anaipeza ngale imodzi ya mtengo wapatali, anapita, nagulitsa zonse anali nazo, naigula imeneyo. Ndiponso, Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi khoka loponyedwa m'nyanja, ndi kusonkhanitsa pamodzi za mitundu yonse; limene podzala, analivuulira pamtunda; ndipo m'mene anakhala pansi, anazisonkhanitsa zabwino m'zotengera, koma zoipa anazitaya kuthengo. Padzatero pa chimaliziro cha nthawi ya pansi pano: angelo adzatuluka, nadzawasankhula oipa pakati pa abwino, nadzawataya m'ng'anjo yamoto; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano. Mwamvetsa zonsezi kodi? Iwo anati kwa Iye, Inde. Ndipo Iye anati kwa iwo, Chifukwa chake, mlembi aliyense, wophunzitsidwa mu Ufumu wa Kumwamba, ali wofanana ndi munthu mwini banja, amene atulutsa m'chuma chake zinthu zakale ndi zatsopano. Ndipo panali, pamene Yesu anatha mafanizo awa, anachokera kumeneko. Ndipo pofika kudziko la kwao, anaphunzitsa iwo m'sunagoge mwao, kotero kuti anazizwa, nanena, Uyu adazitenga kuti nzeru zimenezi ndi zamphamvu izi? Kodi uyu si mwana wa mmisiri wa mitengo? Kodi dzina lake la amake si Maria? Ndi abale ake si Yakobo ndi Yosefe ndi Simoni ndi Yuda? Ndipo alongo ake sali ndife onsewa? Ndipo Iyeyo adazitenga zinthu zonsezi kuti? Ndipo iwo anakhumudwa chifukwa cha Iye. Koma Yesu anati kwa iwo, Mneneri sakhala wopanda ulemu koma kudziko la kwao ndiko, ndi kubanja kwake. Ndipo Iye, chifukwa cha kusakhulupirira kwao, sanachite kumeneko zamphamvu zambiri. Nthawi imeneyo Herode mfumu anamva mbiri ya Yesu, nanena kwa anyamata ake, Uyo ndiye Yohane Mbatizi; anauka kwa akufa; ndipo chifukwa cha ichi zamphamvuzi zilimbalimba mwa iye. Pakuti Herode adamgwira Yohane, nammanga, namuika m'nyumba yandende chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa mbale wake Filipo. Pakuti Yohane ananena kwa iye, Sikuloledwa kwa iwe kukhala naye. Ndipo pofuna kumupha iye, anaopa khamu la anthu, popeza anamuyesa iye mneneri. Koma pakufika tsiku la kubadwa kwake kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodiasi anavina pakati pao, namkondweretsa Herode. Pomwepo iye anamlonjeza chilumbirire, kumpatsa iye chimene chilichonse akapempha. Ndipo iye, atampangira amake, anati, Ndipatseni ine kuno m'mbale mutu wa Yohane Mbatizi. Ndipo mfumuyo anagwidwa ndi chisoni; koma chifukwa cha malumbiro ake, ndi cha iwo anali naye pachakudya, analamulira upatsidwe; ndipo anatumiza mnyamata, namdula mutu Yohane m'nyumba yandende. Ndipo anautenga mutu wake m'mbalemo, naupatsa buthulo: ndipo iye anamuka nao kwa amake. Ndipo ophunzira ake anadza, natola mtembo, nauika; ndipo anadza nauza Yesu. Ndipo Yesu pakumva, anachokera kumeneko m'ngalawa, kunka kumalo achipululu pa yekha; ndipo makamu, pamene anamva, anamtsata Iye mumtunda kuchokera m'midzi. Ndipo Iye anatuluka, naona khamu lalikulu la anthu, nachitira iwo chifundo, nachiritsa akudwala ao. Ndipo pamene panali madzulo, ophunzira ake anafika kwa Iye, nanena, Malo ano nga chipululu, ndipo nthawi yapita tsopano; kauzeni makamuwo amuke, apite kumidzi kukadzigulira okha kamba. Koma Yesu anati kwa iwo, Iwo alibe chifukwa cha kumukira, apatseni ndinu adye. Koma iwo ananena kwa Iye, Ife tilibe kanthu pano koma mikate isanu, ndi nsomba ziwiri. Ndipo Iye anati, Mudze nazo kuno kwa Ine. Ndipo Iye analamulira makamu a anthu akhale pansi paudzu; ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo, ndipo m'mene anayang'ana kumwamba, anadalitsa, nanyema, napatsa mikateyo kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa makamuwo. Ndipo anadya onse, nakhuta; ndipo anatola makombo otsala, nadzala madengu khumi ndi iwiri. Ndipo anadyawo anali amuna monga zikwi zisanu, kuwaleka akazi ndi ana. Ndipo pomwepo Iye anafulumiza ophunzira alowe m'ngalawa, ndi kumtsogolera Iye kutsidya lija, kufikira Iye atauza makamu amuke. Ndipo pamene Iye anawauza makamuwo, anakwera m'phiri pa yekha, kukapemphera: ndipo pamene panali madzulo, Iye anakhala kumeneko yekha. Koma pomwepo ngalawa idafika pakati pa nyanja, yozunzika ndi mafunde; pakuti mphepo inadza mokomana nao. Ndipo pa ulonda wachinai wa usiku, Iye anadza kwa iwo, nayenda pamwamba pa nyanja. Koma m'mene ophunzirawo anamuona Iye, alikuyenda pamadzi, ananthunthumira, nati, Ndi mzukwa! Ndipo anafuula ndi mantha. Koma pomwepo Yesu analankhula nao, nati, Limbani mtima; ndine; musaope. Ndipo Petro anamyankha Iye nati, Ambuye, ngati ndinutu, mundiuze ndidze kwa Inu pamadzi. Ndipo Iye anati, Idza. Ndipo Petro anatsika m'ngalawa, nayenda pamadzi, kufika kwa Yesu. Koma m'mene iye anaiona mphepo, anaopa; ndipo poyamba kumira, anafuula, nati, Ambuye, ndipulumutseni ine! Ndipo pomwepo Yesu anatansa dzanja lake, namgwira iye, nanena naye, Iwe wokhulupirira pang'ono, wakayikiranji mtima? Ndipo pamene iwo analowa m'ngalawamo, mphepo inaleka. Ndipo iwo amene anali m'ngalawamo anamgwadira, nanena, Zoonadi, ndinu Mwana wa Mulungu. Ndipo pamene iwo anaoloka, anafika kumtunda, ku Genesarete. Ndipo m'mene amuna a pamenepo anamzindikira, anatumiza konse kudziko lonse lozungulira, nadza nao kwa Iye onse akukhala ndi nthenda; ndipo anampempha Iye, kuti akhudze yokha mphonje ya chovala chake; ndipo onse amene anamkhudza anachiritsidwa. Pomwepo anadza kwa Yesu Afarisi ndi alembi, ochokera ku Yerusalemu, nati, Ophunzira anu alumphiranji miyambo ya makolo? Pakuti sasamba manja pakudya. Ndipo Iye anayankha, nati kwa iwo, Inunso mulumphiranji lamulo la Mulungu chifukwa cha miyambo yanu? Pakuti Mulungu anati, Lemekeza atate wako ndi amai ako; ndipo, Wakunenera atate wake ndi amake zoipa, afe ndithu. Koma inu munena, Amene aliyense anena kwa atate wake kapena kwa amake, Icho ukanathandizidwa nacho, nchoperekedwa kwa Mulungu; iyeyo sadzalemekeza atate wake. Ndipo inu mupeputsa mau a Mulungu chifukwa cha miyambo yanu. Onyenga inu! Yesaya ananenera bwino za inu, ndi kuti, Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao; koma mtima wao uli kutali ndi Ine. Koma andilambira Ine kwachabe, ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu. Ndipo Iye anaitana makamuwo nati kwa iwo, Imvani, nimudziwitse; si chimene chilowa m'kamwa mwake chiipitsa munthu; koma chimene chituluka m'kamwa mwake, ndicho chiipitsa munthu. Pomwepo anadza ophunzira, nanena kwa Iye, Mudziwa kodi kuti Afarisi anakhumudwa pakumva chonenacho? Koma Iye anayankha nati, Mmera wonse, umene Atate wanga wa Kumwamba sanaubzale, udzazulidwa. Kawalekeni iwo, ali atsogoleri akhungu. Ndipo ngati wakhungu amtsogolera wakhungu, onse awiri adzagwa m'mbuna. Ndipo Petro anayankha nati kwa Iye, Mutifotokozere ife fanizoli. Ndipo Iye anati, Kodi inunso mukhala chipulukirire? Simudziwa kodi kuti zonse zakulowa m'kamwa zipita m'mimba, ndipo zitayidwa kuthengo? Koma zakutuluka m'kamwa zichokera mumtima; ndizo ziipitsa munthu. Pakuti mumtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano; izi ndizo ziipitsa munthu, koma kudya osasamba manja sikuipitsa munthu ai. Ndipo Yesu anatulukapo napatukira kumbali za Tiro ndi Sidoni. Ndipo onani, mkazi wa ku Kanani anatuluka m'malire, nafuula, nati, Mundichitire ine chifundo Ambuye, mwana wa Davide; mwana wanga wamkazi wagwidwa koopsa ndi chiwanda. Koma Iye sanamyankhe mau amodzi. Ndipo ophunzira ake anadza, nampempha, nati, Mumuuze amuke; pakuti afuula pambuyo pathu. Ndipo Iye anayankha, nati, Sindinatumidwa kwa ena koma kwa nkhosa zotayika za banja la Israele. Koma iye anadza, namgwadira Iye, nanena, Ambuye, ndithangateni ine. Ndipo Iye anayankha, nati, Sichabwino kutenga mkate wa ana, ndi kuuponyera tiagalu. Koma iye anati, Etu, Ambuye, pakutinso tiagalu timadya nyenyeswa zakugwa pagome pa ambuye ao. Pomwepo Yesu anayankha, nati kwa iye, Mkaziwe, chikhulupiriro chako ndi chachikulu; chikhale kwa iwe monga momwe wafunira. Ndipo mwana wake anachira nthawi yomweyo. Ndipo Yesu anachoka kumeneko, nadza kunyanja ya Galileya, nakwera m'phiri, nakhala pansi pamenepo. Ndipo makamu ambiri a anthu anadza kwa Iye, ali nao opunduka miyendo, akhungu, osalankhula, opunduka ziwalo, ndi ena ambiri, nawakhazika pansi pa mapazi ake: ndipo Iye anawachiritsa; kotero kuti khamulo linazizwa, pakupenya osalankhula nalankhula, opunduka ziwalo nachira, ndi opunduka miyendo nayenda, ndi akhungu napenya, ndipo iwo analemekeza Mulungu wa Israele. Ndipo Yesu anaitana ophunzira ake, nati, Mtima wanga uchitira chifundo khamu la anthuwa, pakuti ali chikhalire ndi Ine masiku atatu, ndipo alibe kanthu kakudya, ndipo sindifuna kuwauza iwo amuke osadya, kuti angaziye panjira. Ndipo ophunzira ananena kwa Iye, Tiione kuti mikate yotere m'chipululu yakukhutitsa unyinji wotere wa anthu? Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Muli nayo mikate ingati? Ndipo iwo anati, Isanu ndi iwiri, ndi tinsomba pang'ono. Ndipo Iye analamulira anthuwo akhale pansi onse; natenga mikateyo isanu ndi iwiri ndi nsombazo; nayamika Mulungu, nanyema, napatsa kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa anthu. Ndipo onsewa anadya, nakhuta: ndipo anatola makombo otsala madengu asanu ndi awiri odzala. Ndipo anadyawo anali amuna zikwi zinai kuwaleka akazi ndi ana. Ndipo m'mene Iye anauza makamuwo amuke, analowa m'ngalawa, nafika m'malire a Magadani. Ndipo Afarisi ndi Asaduki anadza, namuyesa, namfunsa Iye awaonetse chizindikiro cha Kumwamba. Koma Iye anayankha, nati kwa iwo, Madzulo munena, Kudzakhala ngwee; popeza thambo lili lacheza. Ndipo m'mawa, Lero nkwa mphepo: popeza thambo lili la cheza chodera. Mudziwa kuzindikira za pa nkhope ya thambo; koma zizindikiro za nyengo yino, simungathe kuzindikira. Obadwa oipa ndi achigololo afunafuna chizindikiro; ndipo sadzalandira chizindikiro china, koma chizindikiro cha Yona. Ndipo Iye anawasiya, nachokapo. Ndipo ophunzira anadza kutsidya linalo, naiwala kutenga mikate. Ndipo Yesu anati kwa iwo, Yang'anirani mupewe chotupitsa mkate cha Afarisi ndi Asaduki. Ndipo iwo anafunsana wina ndi mnzake, nati, Sitinatenga mikate. Koma Yesu, m'mene anadziwa, anati, Ha, inu okhulupirira pang'ono, mufunsana chifukwa ninji wina ndi mnzake, kuti simunatenga mikate? Kodi chikhalire simudziwa, ndipo simukumbukira mikate isanu ija ya anthu aja zikwi zisanu, ndi madengu angati munawatola? Penanso mikate isanu ndi iwiri ija ya anthu zikwi zinai, ndi madengu angati munawatola? Bwanji nanga simudziwa kuti sindinanena kwa inu za mikate? Koma pewani chotupitsa cha Afarisi ndi Asaduki. Pomwepo anadziwitsa kuti sanawauze kupeza chotupitsa cha mikate, koma chiphunzitso cha Afarisi ndi Asaduki. Ndipo Yesu, pamene anadza ku dziko la ku Kesareya-Filipi, anafunsa ophunzira ake, kuti, Anthu anena kuti Mwana wa Munthu ndiye yani? Ndipo iwo anati, Ena ati, Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya; ndipo enanso Yeremiya, kapena mmodzi wa aneneri. Iye ananena kwa iwo, Koma inu mutani kuti Ine ndine yani? Ndipo Simoni Petro anayankha nati, Inu ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo. Ndipo Yesu anayankha iye, nati, Ndiwe wodala, Simoni Bara-Yona: pakuti thupi ndi mwazi sizinakuululira ichi, koma Atate wanga wa Kumwamba. Ndiponso Ine ndinena kwa iwe, kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe ili ndidzakhazika Mpingo wanga; ndipo makomo a dziko la akufa sadzagonjetsa uwo. Ndidzakupatsa mafungulo a Ufumu wa Kumwamba; ndipo chimene ukamanga pa dziko lapansi chidzakhala chomangidwa Kumwamba: ndipo chimene ukachimasula pa dziko lapansi, chidzakhala chomasulidwa Kumwamba. Pamenepo analamulira ophunzira kuti asauze munthu kuti Iye ndiye Khristu. Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kuwalangiza ophunzira ake, kuti kuyenera Iye amuke ku Yerusalemu, kukazunzidwa zambiri ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi; ndi kukaphedwa, ndi tsiku lachitatu kuuka kwa akufa. Ndipo Petro anamtenga Iye, nayamba kumdzudzula, kuti, Dzichitireni chifundo, Ambuye; sichidzatero kwa Inu ai. Koma Iye anapotoloka, nati kwa Petro, Pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; ndiwe chondikhumudwitsa Ine; chifukwa sumasamalira za Mulungu, koma za anthu. Pomwepo Yesu anati kwa ophunzira ake, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wake, nanditsate Ine. Pakuti iye amene afuna kupulumutsa moyo wake adzautaya: koma iye amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine, adzaupeza. Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wake? Kapena munthu adzaperekanji chosintha ndi moyo wake? Pakuti Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate wake, pamodzi ndi angelo ake; ndipo pomwepo Iye adzabwezera kwa anthu onse monga machitidwe ao. Indetu ndinena kwa inu, kuti alipo ena a iwo aima pano sadzalawa ndithu imfa, kufikira adzaona Mwana wa Munthu atadza mu ufumu wake. Ndipo atapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu anatenga Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane mbale wake, napita nao pa okha pa phiri lalitali; ndipo Iye anasandulika pamaso pao; ndipo nkhope yake inawala monga dzuwa, ndi zovala zake zinakhala zoyera mbu monga kuwala. Ndipo onani, Mose ndi Eliya anaonekera kwa iwo, alinkulankhula ndi Iye. Ndipo Petro anayankha, nati kwa Yesu, Ambuye, kuli bwino kuti ife tikhale pano; ngati mulola ndidzamanga pano misasa itatu; umodzi wa Inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya. Akali chilankhulire, onani, mtambo wowala unawaphimba iwo: ndipo onani, mau ali kunena mumtambo, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani Iye. Ndipo pamene ophunzira anamva, anagwa nkhope zao pansi, naopa kwakukulu. Ndipo Yesu anadza, nawakhudza nati, Ukani, musaopa. Ndipo iwo, pokweza maso ao sanaone munthu, koma Yesu yekha. Ndipo pamene anali kutsika paphiri, Yesu anawalamula iwo kuti, Musakauze munthu choonekacho, kufikira Mwana wa Munthu adadzauka kwa akufa. Ndipo ophunzira ake anamfunsa, nanena, Ndipo bwanji alembi amanena kuti Eliya ndiye atsogole kudza? Ndipo Iye anayankha, nati, Eliya akudzatu, nadzabwezera zinthu zonse; koma ndinena kwa inu, kuti Eliya anadza kale, ndipo iwo sanamdziwe iye, koma anamchitira zonse zimene anazifuna iwo. Ndipo chonchonso Mwana wa Munthu adzazunzidwa ndi iwo. Pomwepo ophunzira anazindikira kuti analankhula nao za Yohane Mbatizi. Ndipo pamene iwo anadza kukhamu la anthu, kunafika kwa Iye munthu, namgwadira Iye, nati, Ambuye, chitirani mwana wanga chifundo; chifukwa adwala nkhunyu, kuzunzika koipa: pakuti amagwa kawirikawiri pamoto, ndi kawirikawiri m'madzi. Ndipo ndinadza naye kwa ophunzira anu, koma iwo sanathe kumchiritsa. Ndipo Yesu anayankha nati, Ha, obadwa osakhulupirira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji? Ndidzalekerera inu nthawi yanji? Mudze naye kwa Ine kuno. Ndipo Yesu anamdzudzula; ndipo chiwanda chinatuluka mwa iye; ndipo mnyamatayo anachira kuyambira nthawi yomweyo. Pamenepo ophunzira anadza kwa Yesu, ali pa yekha, nati, Nanga ife sitinakhoza bwanji kuchitulutsa? Ndipo Iye ananena kwa iwo, Chifukwa chikhulupiriro chanu nchaching'ono: pakuti indetu ndinena kwa inu, Mukakhala nacho chikhulupiriro monga kambeu kampiru, mudzati ndi phiri ili, Senderapo umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakukanikani. *** Ndipo m'mene anali kutsotsa m'Galileya, Yesu ananena nao, Mwana wa Munthu adzaperekedwa m'manja a anthu; ndipo adzamupha Iye, ndipo Iye adzauka tsiku lachitatu. Ndipo iwo anali ndi chisoni chachikulu. Ndipo pofika ku Kapernao amene aja akulandira ndalama za ku Kachisi anadza kwa Petro nati, Kodi Mphunzitsi wanu sapereka rupiyalo? Iye anavomera, Apereka. Ndipo polowa iye m'nyumba, Yesu anatsogola kunena naye, nati, Simoni, uganiza bwanji? Mafumu a dziko lapansi alandira msonkho kwa yani? Kwa ana ao kodi, kapena kwa akunja? Ndipo m'mene iye anati, Kwa akunja, Yesu ananena kwa iye, Chifukwa chake anawo ali aufulu. Koma kuti ife tisawakhumudwitse, pita iwe kunyanja, ukaponye mbedza, nuitole nsomba yoyamba kuwedza; ndipo ukaikanula pakamwa pake udzapezamo rupiya; tatenga limeneli, nuwapatse ilo pamtu pa iwe ndi Ine. Nthawi yomweyo ophunzira anadza kwa Yesu, nanena, Ndani kodi ali wopambana mu Ufumu wa Kumwamba? Ndipo pamene Yesu anaitana kamwana, anakaimitsa pakati pao, nati, Indetu ndinena kwa inu, Ngati simutembenuka, nimukhala monga tianato, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba. Chifukwa chake yense amene adzichepetsa yekha monga kamwana aka, yemweyo ali wopambana mu Ufumu wa Kumwamba. Ndipo amene adzalandira kamwana kamodzi kotereka chifukwa cha dzina langa, alandira Ine; koma yense amene adzakhumudwitsa kamodzi ka tiana iti, takukhulupirira Ine, kumuyenera iye kuti mphero yaikulu ikolowekedwe m'khosi mwake, namizidwe poya pa nyanja. Tsoka lili ndi dziko lapansi chifukwa cha zokhumudwitsa! Pakuti sikutheka kuti zokhumudwitsa zileke kudza, koma tsoka lili ndi munthu amene chokhumudwitsacho chidza ndi iye. Ndipo ngati dzanja lako, kapena phazi lako likukhumudwitsa iwe, ulidule, nulitaye; nkwabwino, kuti ulowe m'moyo wopunduka dzanja kapena phazi, koposa kuponyedwa m'moto wa nthawi zonse, uli ndi manja awiri kapena mapazi awiri. Ndipo ngati diso lako likukhumudwitsa, ulikolowole, nulitaye: nkwabwino kuti ulowe m'moyo ndi diso limodzi koposa kuponyedwa m'Gehena wamoto, uli ndi maso awiri. Yang'anirani kuti musanyoze mmodzi wa ang'ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kuti angelo ao apenya chipenyere nkhope ya Atate wanga wa Kumwamba. *** Nanga muyesa bwanji? Ngati munthu ali nazo nkhosa makumi khumi, ndipo ikasokera imodzi ya izo, kodi saleka zija makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi zinai, napita kumapiri, kukafuna yosokerayo? Ndimo akaipeza, indedi ndinena kwa inu, akondwera nayo koposa ndi makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi zinai zosasokera. Chomwecho sichili chifuniro cha Atate wanu wa Kumwamba kuti mmodzi wa ang'ono awa atayike. Ndipo ngati mbale wako akuchimwira iwe, pita, numlangize pa nokha iwe ndi iye; ngati akumvera iwe, wambweza mbale wako. Koma ngati samvera, onjeza kutenga ndi iwe wina mmodzi kapena awiri, kuti atsimikizidwe mau onse pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu. Ndipo ngati iye samvera iwo, uuze Mpingo; ndipo ngati iye samveranso Mpingowo, akhale kwa iwe monga wakunja ndi wamsonkho. Indetu ndinena kwa inu, Zilizonse mukazimanga pa dziko lapansi zidzakhala zomangidwa Kumwamba: ndipo zilizonse mukazimasula pa dziko lapansi, zidzakhala zomasulidwa Kumwamba. Ndiponso ndinena kwa inu kuti ngati awiri a inu avomerezana pansi pano chinthu chilichonse akachipempha, Atate wanga wa Kumwamba adzawachitira. Pakuti kumene kuli awiri kapena atatu asonkhanira m'dzina langa, ndili komweko pakati pao. Pamenepo Petro anadza, nati kwa Iye, Ambuye, mbale wanga adzandilakwira kangati, ndipo ine ndidzamkhululukira iye? Kufikira kasanu ndi kawiri kodi? Yesu ananena kwa iye, Sindinena kwa iwe kufikira kasanu ndi kawiri, koma kufikira makumi asanu ndi awiri kubwerezedwa kasanu ndi kawiri. Chifukwa chake Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu, mfumu, amene anafuna kuwerengera nao akapolo ake. Ndipo pamene anayamba kuwerengera, anadza kwa iye ndi wina wamangawa wa ndalama za matalente zikwi khumi. Koma popeza iye anasowa kanthu kombwezera, mbuye wake analamulira kuti iye agulitsidwe, ndi mkazi wake ndi ana ake omwe, ndi zonse ali nazo, kuti akabwezedwe mangawawo. Chifukwa chake kapoloyo anagwada pansi, nampembedzera, nati, Mbuye, bakandiyembekezani ine, ndipo zonse ndidzazibwezera kwa inu. Ndipo mbuye wa kapoloyo anagwidwa ndi chisoni mumtima, nammasula iye, namkhululukira ngongole. Koma kapolo uyu, potuluka anapeza wina wa akapolo anzake yemwe anamkongola iye marupiya atheka makumi khumi, namgwira, namkanyanga pakhosi, nati, Bwezera chija unachikongola. Pamenepo kapolo mnzakeyu anagwada pansi, nampempha iye, nati, Bakandiyembekeza ine, ndipo ndidzakubwezera. Ndipo iye sanafune; koma anamuka, namponya iye m'nyumba yandende, kufikira abwezere ngongole. Chifukwa chake m'mene akapolo anzake anaona zochitidwazo, anagwidwa chisoni chachikulu, nadza, nalongosolera mbuye wao zonse zimene zinachitidwa. Pomwepo mbuye wake anamuitana iye, nanena naye, Kapolo iwe woipa, ndinakukhululukira iwe mangawa onse aja momwe muja unandipempha ine; kodi iwenso sukadamchitira kapolo mnzako chisoni, monga inenso ndinakuchitira iwe chisoni? Ndipo mbuye wake anakwiya, nampereka kwa azunzi, kufikira akambwezere iye mangawa onse. Chomwechonso Atate wanga a Kumwamba adzachitira inu, ngati inu simukhululukira yense mbale wake ndi mitima yanu. Ndipo panali pamene Yesu anatha mau amenewa, anachokera ku Galileya, nadza ku malire a Yudeya, a ku tsidya lija la Yordani. Ndipo makamu akulu a anthu anamtsata; ndipo Iye anawachiritsa kumeneko. Ndipo Afarisi anadza kwa Iye, namuyesa, nanena, Kodi nkuloledwa kuti munthu achotse mkazi wake pa chifukwa chilichonse? Ndipo Iye anayankha, nati, Kodi simunawerenga kuti Iye amene adalenga anthu pachiyambi, anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi, nati, Chifukwa cha ichi mwamuna adzasiya atate wake ndi amake, nadzaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi? Chotero kuti salinso awiri koma thupi limodzi. Chifukwa chake ichi chimene Mulungu anachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse. Iwo ananena kwa Iye, Nanga chifukwa ninji Mose analamula kupatsa kalata wa chilekaniro, ndi kumchotsa? Iye ananena kwa iwo, Chifukwa cha kuuma mtima kwanu, Mose anakulolezani kuchotsa akazi anu; koma pachiyambi sikunakhala chomwecho. Ndipo Ine ndinena kwa inu, Amene aliyense akachotsa mkazi wake, kosakhala chifukwa cha chigololo, nadzakwatira wina, achita chigololo: ndipo iye amene akwatira wochotsedwayo, achita chigololo. Ophunzira ananena kwa Iye, Ngati mlandu wa munthu ndi mkazi wake uli wotere, sikuli kwabwino kukwatira. Koma Iye anati kwa iwo, Onse sangathe kulandira chonena ichi, koma kwa iwo omwe chapatsidwa. Pakuti pali osabala, amene anabadwa otero m'mimba ya amao: ndipo pali osabala anawafula anthu; ndipo pali osabala amene anadzifula okha, chifukwa cha Ufumu wa Kumwamba. Amene angathe kulandira ichi achilandire. Pamenepo anadza nato tiana kwa Iye, kuti Iye aike manja ake pa ito, ndi kupemphera: koma ophunzirawo anawadzudzula. Koma Yesu anati, Tilekeni tiana, musatikanize kudza kwa Ine: chifukwa Ufumu wa Kumwamba uli wa totere. Ndipo Iye anaika manja ake pa ito, nachokapo. Ndipo onani, munthu anadza kwa Iye, nati, Mphunzitsi, chabwino nchiti ndichichite, kuti ndikhale nao moyo wosatha? Ndipo Iye anati kwa iye, Undifunsiranji za chinthu chabwino? Alipo Mmodzi ndiye wabwino: koma ngati ufuna kulowa m'moyo, sunga malamulo. Iye ananena kwa Iye, Otani? Ndipo Yesu anati, Usaphe, Usachite chigololo, Usabe, Usachite umboni wonama, Lemekeza atate wako ndi amai ako, ndipo, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini. Mnyamatayo ananena kwa Iye, Zonsezi ndinazisunga, ndisowanso chiyani? Yesu ananena naye, Ngati ufuna kukhala wangwiro, pita, kagulitse zomwe uli nazo, nupatse aumphawi, ndipo udzakhala ndi chuma Kumwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate. Koma mnyamatayo m'mene anamva chonenacho, anamuka wachisoni; pakuti anali nacho chuma chambiri. Ndipo Yesu anati kwa ophunzira ake, Indetu ndinena kwa inu, kuti munthu mwini chuma adzalowa movutika mu Ufumu wa Kumwamba. Ndiponso ndinena kwa inu, Nkwapafupi kuti ngamira ipyole diso la singano, koposa mwini chuma kulowa Ufumu wa Kumwamba. Ndipo ophunzira, pamene anamva, anazizwa kwambiri, nanena, Ngati nkutero angapulumuke ndani? Ndipo Yesu anawayang'ana, nati kwa iwo, Ichi sichitheka ndi anthu, koma zinthu zonse zitheka ndi Mulungu. Pomwepo Petro anayankha, nati kwa Iye, onani, ife tinasiya zonse ndi kutsata Inu; nanga tsono tidzakhala ndi chiyani? Ndipo Yesu anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti inu amene munanditsata Ine, m'kubadwanso, pamene Mwana wa Munthu adzakhala pa chimpando cha ulemerero wake, inunso, mudzakhala pa mipando khumi ndi iwiri, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israele. Ndipo onse amene adasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amai, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha dzina langa, adzalandira zobwezeredwa zambirimbiri, nadzalowa moyo wosatha. Koma ambiri oyamba adzakhala akuthungo, ndi akuthungo adzakhala oyamba. Pakuti Ufumu wa Kumwamba ufanana ndi munthu mwini banja, amene anatuluka mamawa kukalembera antchito a m'munda wake wampesa. Ndipo pamene adapangana ndi antchito, pa rupiya latheka limodzi tsiku limodzi, anawatumiza kumunda wake. Ndipo anatuluka dzuwa litakwera, naona ena ataima chabe pabwalo; ndipo kwa iwo anati, Pitani inunso kumunda, ndipo ndidzakupatsani chimene chili choyenera. Ndipo iwo anapita. Ndiponso anatuluka usana, ndimonso popendeka dzuwa, nachita chimodzimodzi. Ndipo poyandikira madzulo anatuluka, napeza ena ataima; nanena kwa iwo, Mwaimiranji kuno dzuwa lonse chabe? Iwo ananena kwa iye, Chifukwa palibe munthu anatilemba. Iye anati kwa iwo, Pitani inunso kumundawo wampesa. Ndipo pamadzulo, mwini munda anati kwa kapitao wake, Kaitane antchito, nuwapatse iwo kulipira kwao, uyambe kwa omalizira kufikira kwa oyamba. Ndipo pamene iwo olembedwa poyandikira madzulo anadza, analandira munthu aliyense rupiya latheka limodzi. Ndipo m'mene oyamba anadza, analingalira kuti adzalandira kopambana, ndipo iwonso analandira onse rupiya latheka. Koma m'mene iwo analilandira, anaderera kwa mwini banja, nati, Omalizira awa anagwira ntchito mphindi yaing'ono, ndipo munawalinganiza ndi ife amene tinapirira kuwawa kwa dzuwa ndi kutentha kwake. Koma iye anayankha, nati kwa mmodzi wa iwo, Mnzanga, sindikunyenga iwe; kodi iwe sunapangana ndi ine pa rupiya latheka limodzi? Tenga lako, numuke; pakuti ine ndifuna kupatsa kwa uyu womalizira monga kwa iwe. Sikuloleka kwa ine kodi kuchita chimene ndifuna ndi zanga? Kapena diso lako laipa kodi chifukwa ine ndili wabwino? Chomwecho omalizira adzakhala oyamba, ndipo oyamba adzakhala omalizira. Ndipo pamene Yesu analikukwera ku Yerusalemu, anatenga ophunzira khumi ndi awiri napita nao pa okha, ndipo panjira anati kwa iwo, Onani, tikwera ku Yerusalemu; ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi, ndipo iwo adzamweruza kuti ayenera imfa, nadzampereka kwa anthu akunja kuti amnyoze ndi kumkwapula, ndi kumpachika; ndipo Iye adzaukitsidwa tsiku lachitatu. Pomwepo anadza kwa Iye amake a ana a Zebedeo ndi ana ake omwe, namgwadira, ndi kumpempha kanthu. Ndipo Iye anati kwa iye, Ufuna chiyani? Iye ananena, Lamulirani kuti ana anga awiri amenewa adzakhale, wina ku dzanja lanu lamanja, ndi wina kulamanzere, mu ufumu wanu. Koma Yesu anayankha nati, Inu simudziwa chimene mupempha. Kodi mukhoza kumwera chikho nditi ndidzamwere Ine? Iwo ananena kwa Iye, Ife tikhoza. Iye ananena kwa iwo, Chikho changa mudzamweradi; koma kukhala kudzanja lamanja kwanga ndi kulamanzere, sikuli kwanga kupatsa, koma kuli kwa iwo omwe kwakonzedweratu ndi Atate wanga. Ndipo m'mene khumiwo anamva, anapsa mtima ndi abale awiriwo. Koma Yesu anawaitana, nati, Mudziwa kuti mafumu a anthu amadziyesa okha ambuye ao, ndipo akulu ao amachita ufumu pa iwo. Sikudzakhala chomwecho kwa inu ai; koma amene aliyense akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu; ndipo amene aliyense akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu: monga Mwana wa Munthu sanadze kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri. Ndipo pamene iwo analikutuluka m'Yeriko, khamu lalikulu la anthu linamtsata Iye. Ndipo onani, anthu akhungu awiri anakhala m'mphepete mwa njira; m'mene iwo anamva kuti Yesu analikupitirirapo, anafuula nati, Mutichitire ife chifundo, Inu Mwana wa Davide. Ndipo khamulo linawaletsa, kuti atonthole: koma anakuwitsa, nanena, Ambuye, mutichitire chifundo, Inu Mwana wa Davide. Ndipo Yesu anaima, nawaitana, nati, Mufuna kuti ndikuchitireni chiyani? Ananena kwa Iye, Ambuye, kuti maso athu apenye. Ndipo Yesu anagwidwa ndi chifundo, nakhudza maso ao; ndipo pomwepo anapenyanso, namtsata Iye. Ndipo pamene iwo anayandikira ku Yerusalemu, nafika ku Betefage, kuphiri la Azitona, pamenepo Yesu anatumiza ophunzira awiri, nanena kwa iwo, Mukani kumudzi wopenyana ndi inu, ndipo pomwepo mudzapeza bulu womangidwa, ndi mwana wake pamodzi naye, masulani iwo, mudze nao kwa Ine. Ndipo munthu akanena kanthu ndi inu, mudzati, Ambuye asowa iwo, ndipo pomwepo adzawatumiza. Ndipo ichi chinatero, kuti chikachitidwe chonenedwa ndi mneneri kuti, Tauzani mwana wamkazi wa Ziyoni, Taona, mfumu yako idza kwa iwe, wofatsa ndi wokwera pa bulu, ndi pa kabulu, mwana wa nyama yonyamula katundu. Ndipo ophunzirawo anamuka, nachita monga Yesu anawauza; nabwera ndi bulu ndi mwana wake, naika pa iwo zovala zao, nakhala Iye pamenepo. Ndipo ambirimbiri a mpingowo anayala zovala zao panjira; ndipo ena anadula nthambi za mitengo, naziyala m'njiramo. Ndipo mipingo yakumtsogolera ndi yakumtsatira, inafuula, kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide! Wolemekezeka ndiye wakudza m'dzina la Ambuye! Hosana m'Kumwambamwamba! Ndipo m'mene adalowa m'Yerusalemu mudzi wonse unasokonezeka, nanena, Ndani uyu? Ndipo makamu a anthu anati, Uyu ndi mneneri Yesu wa ku Nazarete wa ku Galileya. Ndipo Yesu analowa ku Kachisi wa Mulungu natulutsira kunja onse akugulitsa ndi kugula malonda, nagubuduza magome a osintha ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda; nanena kwa iwo, Chalembedwa, Nyumba yanga idzanenedwa nyumba yakupemphera; koma inu mwaiyesa phanga la achifwamba. Ndipo anadza kwa Iye ku Kachisiko akhungu ndi opunduka miyendo, nachiritsidwa. Koma ansembe aakulu ndi alembi, m'mene anaona zozizwitsa zomwe Iye anazichita, ndi ana alinkufuula ku Kachisiko kuti, Hosana kwa Mwana wa Davide, anapsa mtima, nanena kwa Iye, Mulinkumva kodi chimene alikunena awa? Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Inde: simunawerenga kodi, M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza? Ndipo Iye anawasiya, natuluka m'mzinda, napita ku Betaniya, nagona kumeneko. Ndipo mamawa, m'mene Iye analinkunkanso kumzinda, anamva njala. Ndipo pakuona mkuyu umodzi panjira, anafika pamenepo, napeza palibe kanthu koma masamba okhaokha; nati Iye kwa uwo, Sudzabalanso chipatso kunthawi zonse. Ndipo pomwepo mkuyuwo unafota. Ndipo ophunzira poona ichi anazizwa, nati, Mkuyuwo unafota bwanji msanga? Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Indedi ndinena kwa inu, Ngati mukhala nacho chikhulupiriro, osakayikakayika, mudzachita si ichi cha pa mkuyu chokha, koma ngati mudzati ngakhale kuphiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nyanja, chidzachitidwa. Ndipo zinthu zilizonse mukazifunsa m'kupemphera ndi kukhulupirira, mudzazilandira. Ndipo m'mene Iye analowa m'Kachisi, ansembe aakulu ndi akulu a anthu anadza kwa Iye analikuphunzitsa, nanena, Muchita izi ndi ulamuliro wotani? Ndipo ndani anakupatsani ulamuliro wotere? Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Inenso ndikufunsani mau amodzi, amene ngati mundiuza, Inenso ndikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizichita izi: Ubatizo wa Yohane, uchokera kuti? Kumwamba kodi kapena kwa anthu? Koma iwo anafunsana wina ndi mnzake, kuti, Tikati, Kumwamba, Iye adzati kwa ife, Munalekeranji kumvera iye? Koma tikati, Kwa anthu, tiopa khamulo la anthu; pakuti onse amuyesa Yohane mneneri. Ndipo anamyankha Yesu, nati, Sitidziwa ife. Iyenso ananena nao, Inenso sindikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizichita izi. Nanga mutani? Munthu anali nao ana awiri; nadza iye kwa woyamba nati, Mwanawe, kagwire lero ntchito kumunda wampesa. Koma iye anakana, nati, Sindifuna ine; koma pambuyo pake analapa mtima napita. Ndipo anadza kwa winayo, natero momwemo. Ndipo iye anavomera, nati, Ndipita mbuye; koma sanapite. Ndani wa awiriwo anachita chifuniro cha atate wake? Iwo ananena, Woyambayo. Yesu ananena kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti amisonkho ndi akazi achiwerewere amatsogolera inu, kulowa mu Ufumu wa Kumwamba. Popeza Yohane anadza kwa inu m'njira ya chilungamo, ndipo simunamvera iye; koma amisonkho ndi akazi achiwerewere anammvera iye; ndipo inu, m'mene munachiona, simunalapa pambuyo pake, kuti mumvere iye. Mverani fanizo lina: Panali munthu, mwini banja, amene analima munda wamphesa, nauzunguniza linga, nakumba umo moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa olima munda, namuka kwina. Ndipo pamene nyengo ya zipatso inayandikira, anatumiza akapolo ake kwa olima mundawo, kukalandira zipatso zake. Ndipo olimawo anatenga akapolo ake, nampanda mmodzi, wina namupha, wina namponya miyala. Anatumizanso akapolo ena, akuchuluka oposa akuyambawa; ndipo anawachitira iwo momwemo. Koma pambuyo pake anatumiza kwa iwo mwana wake, nati, Adzachitira mwana wanga ulemu. Koma olimawo m'mene anaona mwanayo, ananena wina ndi mnzake, Uyo ndiye wolowa; tiyeni, timuphe, ndipo ife tidzatenga cholowa chake. Ndipo anamtenga iye, namponya kunja kwa munda, namupha. Tsono atabwera mwini munda, adzachitira olimawo chiyani? Iwo ananena kwa Iye, Adzaononga koipa oipawo, nadzapereka mundawo kwa olima ena, amene adzambwezera iye zipatso pa nyengo zake. Yesu ananena kwa iwo, Kodi simunawerenga konse m'malembo, Mwala umene anaukana omanga nyumba womwewu unakhala mutu wa pangodya: Ichi chinachokera kwa Ambuye, ndipo chili chozizwitsa m'maso mwathu? Chifukwa chake ndinena kwa inu, Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu, nudzapatsidwa kwa anthu akupatsa zipatso zake. Ndipo iye wakugwa pa mwala uwu adzaphwanyika; koma pa iye amene udzamgwera, udzampera iye. Ndipo ansembe aakulu ndi Afarisi, pakumva mafanizo ake, anazindikira kuti alikunena za iwo. Ndipo pamene anafuna kumgwira, anaopa makamu a anthu, chifukwa anamuyesa mneneri. Ndipo Yesu anayankha, nalankhulanso kwa iwo m'mafanizo, nati, Ufumu wa Kumwamba ufanafana ndi munthu, mfumu, amene anakonzera mwana wake phwando la ukwati, natumiza akapolo ake kukaitana oitanidwa kuukwati umene; ndipo iwo sanafune kudza. Pomwepo anatumizanso akapolo ena, nanena, Uzani oitanidwawo, Onani, ndakonza phwando langa; ng'ombe zanga, ndi zonona ndinazipha, ndi zinthu zonse zapsa: idzani kuukwati. Koma iwo ananyalanyaza, nachoka, wina kumunda wake, wina kumalonda ake: ndipo otsala anagwira akapolo ake, nawachitira chipongwe, nawapha. Koma mfumu inakwiya; nituma asilikali ake napululutsa ambanda aja, nitentha mudzi wao. Pomwepo inanena kwa akapolo ake, Za ukwati tsopano zapsa, koma oitanidwawo sanayenera. Chifukwa chake pitani inu kumphambano za njira, ndipo amene aliyense mukampeze, itanani kuukwatiku. Ndipo akapolo ao anatulukira kunjira, nasonkhanitsa onse amene anawapeza, ngakhale oipa, ngakhale abwino; ndipo ukwatiwo unadzala ndi okhala pachakudya. Koma mfumuyo m'mene inadza kuwaona akudyawo, anapenya momwemo munthu wosavala chovala cha ukwati; nanena kwa iye, Mnzangawe, unalowa muno bwanji wosakhala nacho chovala cha ukwati? Ndipo iye analibe mau. Pomwepo mfumu inati kwa atumiki, Mumange iye manja ndi miyendo, mumponye kumdima wakunja; komweko kudzali kulira ndi kukukuta mano. Pakuti oitanidwa ndiwo ambiri, koma osankhidwa ndiwo owerengeka. Pomwepo Afarisi anamuka, nakhala upo wakumkola Iye m'kulankhula kwake. Ndipo anatumiza kwa Iye ophunzira ao, pamodzi ndi Aherode, amene ananena, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli woona, ndipo muphunzitsa njira ya Mulungu moona ndithu, ndipo simusamala munthu aliyense; pakuti simuyang'anira pa nkhope ya anthu. Chifukwa chake mutiuze ife, muganiza chiyani? Kuloledwa kodi kupatsa msonkho kwa Kaisara, kapena iai? Koma Yesu anadziwa kuipa kwao, nati, Mundiyeseranji Ine, onyenga inu? Tandionetsani Ine ndalama yamsonkho. Ndipo iwo anadza nalo kwa Iye rupiya latheka. Ndipo Iye anati kwa iwo, Ncha yani chithunzithunzi ichi, ndi kulemba kwake? Nanena iwo, Cha Kaisara. Pomwepo Iye anati kwa iwo, Chifukwa chake patsani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu. Ndipo pamene iwo anamva, anazizwa, namsiya Iye, nachokapo. Tsiku lomwelo anadza kwa Iye Asaduki, amene amanena kuti palibe kuuka kwa akufa; namfunsa Iye, nanena, Mphunzitsi, Mose anati, Ngati munthu akafa wopanda mwana, mphwake adzakwatira mkazi wake, nadzamuukitsira mbale wake mbeu. Tsono panali ndi ife abale asanu ndi awiri; ndipo wakuyamba anakwatira, namwalira wopanda mbeu, nasiyira mphwake mkazi wake; chimodzimodzi wachiwiri, ndi wachitatu, kufikira wachisanu ndi chiwiri. Ndipo pomalizira anamwaliranso mkaziyo. Chifukwa chake m'kuuka kwa akufa, iye adzakhala mkazi wa yani wa asanu ndi awiriwo? Pakuti onse anakhala naye. Koma Yesu anayankha, nati kwa iwo, Mungolakwa osadziwa malembo, kapena mphamvu za Mulungu. Pakuti m'kuuka kwa akufa sakwatira, kapena kukwatiwa, koma akhala ngati angelo a Kumwamba. Koma za kuuka kwa akufa, simunawerenga kodi chomwe chinanenedwa kwa inu ndi Mulungu, kuti, Ine ndili Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo? Sali Mulungu wa akufa koma wa amoyo. Ndipo pamene makamu a anthu anamva, anazizwa ndi chiphunzitso chake. Koma Afarisi, pakumva kuti Iye anatontholetsa Asaduki, anasonkhana. Ndipo mmodzi wa iwo, mphunzitsi wa chilamulo, anamfunsa ndi kumuyesa Iye, nati, Mphunzitsi, lamulo lalikulu ndi liti la m'chilamulo? Ndipo Yesu anati kwa iye, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. Ili ndilo lamulo lalikulu ndi loyamba. Ndipo lachiwiri lolingana nalo ndili, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini. Pa malamulo awa awiri mpokolowekapo chilamulo chonse ndi aneneri. Ndipo pamene Afarisi anasonkhana, Yesu anawafunsa, nati, Muganiza bwanji za Khristu? Ali mwana wa yani? Iwo ananena kwa Iye, Wa Davide. Iye anati kwa iwo, Ndipo Davide mu Mzimu amtchula Iye bwanji Ambuye, nanena, Ambuye ananena kwa Ambuye wanga, ukhale pa dzanja lamanja langa, kufikira Ine ndidzaika adani ako pansi pa mapazi ako. Chifukwa chake ngati Davide amtchula Iye Ambuye, ali mwana wake bwanji? Ndipo panalibe mmodzi anatha kumyankha mau. Ndipo sanalimbike mtima munthu aliyense kumfunsa kanthu kuyambira tsiku lomwelo. Pomwepo Yesu analankhula ndi makamu a anthu ndi ophunzira ake, nanena, Alembi ndi Afarisi akhala pa mpando wa Mose; chifukwa chake zinthu zilizonse zimene iwo akauza inu, chitani nimusunge; koma musatsanza ntchito zao; pakuti iwo amalankhula, koma samachita. Inde, amanga akatundu olemera ndi osautsa ponyamula, nawasenza pa mapewa a anthu; koma iwo eni okha safuna kuwasuntha amenewo ndi chala chao. Koma amachita ntchito zao zonse kuti aonekere kwa anthu; pakuti akulitsa chitando chake cha njirisi zao, nakulitsa mphonje, nakonda malo a ulemu pamaphwando, ndi mipando ya ulemu m'masunagoge, ndi kulonjeredwa m'misika, ndi kutchedwa ndi anthu, Rabi. Koma inu musatchedwa Rabi; pakuti Mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale. Ndipo inu musatchule wina atate wanu pansi pano, pakuti alipo mmodzi ndiye Atate wanu wa Kumwamba. Ndipo musatchedwa atsogoleri, pakuti alipo mmodzi Mtsogoleri wanu, ndiye Khristu. Koma wamkulu wopambana wa inu adzakhala mtumiki wanu. Ndipo amene aliyense akadzikuza yekha adzachepetsedwa; koma amene adzichepetsa mwini yekha adzakulitsidwa. Koma tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pao; pakuti inu nokha simulowamo, ndipo muwaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo. *** Tsoka inu alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mupitapita kunyanja ndi kumtunda kuyesa munthu mmodzi mtembenuki; ndipo m'mene akhala wotere, mumsandutsa mwana wa Gehena woposa inu kawiri. Tsoka inu, atsogoleri akhungu, amene munena, Amene aliyense akalumbira kutchula Kachisi, palibe kanthu; koma amene akalumbira kutchula golide wa Kachisi, wadzimangirira. Inu opusa, ndi akhungu: pakuti choposa nchiti, golide kodi, kapena Kachisi amene ayeretsa golideyo? Ndiponso, Amene aliyense akalumbira kutchula guwa la nsembe, palibe kanthu; koma amene akalumbira kutchula mtulo wa pamwamba pake wadzimangirira. Inu akhungu, pakuti choposa nchiti, mtulo kodi, kapena guwa la nsembe limene liyeretsa mtulowo? Chifukwa chake wakulumbira kutchula guwa la nsembe, alumbira limenelo ndi zonse za pamwamba pake. Ndipo wakulumbira kutchula Kachisi, alumbira ameneyo ndi Iye wakukhala momwemo. Ndipo wakulumbira kutchula Kumwamba, alumbira chimpando cha Mulungu, ndi Iye wakukhala pomwepo. Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi katsabola, ndi la chitowe, nimusiya zolemera za chilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kuchitira chifundo, ndi chikhulupiriro; koma zijazo munayenera kuzichita, osasiya izi zomwe. Atsogoleri akhungu inu, akukuntha udzudzu, koma mumeza ngamira. Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsuka kunja kwake kwa chikho ndi mbale, koma m'katimo iwo adzala ndi kulanda ndi kusadziletsa. Mfarisi iwe wakhungu, yambotsuka m'kati mwa chikho ndi mbale, kuti kunja kwake kukhalenso koyera. Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mufanafana ndi manda opaka njereza, amene aonekera okoma kunja kwake, koma adzala m'katimo ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse. Chomwecho inunso muonekera olungama pamaso pa anthu, koma m'kati muli odzala ndi chinyengo ndi kusaweruzika. Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mumanga nyumba za pa manda a aneneri, ndipo mukonza manda a anthu olungama, ndi kuti, Ife tikadakhala m'masiku a makolo anthu, sitikadakhala oyanjana nao pa mwazi wa aneneri. Pomwepo mutsimikiza nokha, kuti muli ana a iwo amene anapha aneneri. Dzazani inu muyeso wa makolo anu. Njoka inu, obadwa inu a mamba, mudzatha bwanji kuthawa kulanga kwake kwa Gehena? Chifukwa cha icho, onani, ndituma kwa inu aneneri ndi anzeru ndi alembi; ena a iwo mudzawapha, mudzawapachika; ndi ena a iwo mudzawakwapula m'masunagoge mwanu, ndi kuwazunza, kuchokera kumudzi umodzi, kufikira kumudzi wina; kotero kuti udzafika pa inu mwazi wonse wotayidwa pa dziko lapansi, kuyambira kumwazi wa Abele wolungamayo, kufikira kumwazi wa Zekariya mwana wa Barakiya, amene munamupha pakati pa Kachisi ndi guwa la nsembe. Indetu ndinena kwa inu, Zinthu zonse izi zidzafika pa mbadwo uwu wamakono. Ha, Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo otumidwa kwa iwe! Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m'mapiko ake, koma inu simunafuna ai! Onani, nyumba yanu yasiyidwa kwa inu yabwinja. Pakuti ndinena kwa inu, Simudzandionanso Ine, kuyambira tsopano, kufikira mudzanena, Wolemekezedwa Iye amene akudza m'dzina la Ambuye. Ndipo Yesu anatuluka ku Kachisi; ndipo ophunzira ake anadza kudzamuonetsa chimangidwe cha Kachisiyo. Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Simuona izi zonse kodi? Indetu ndinena kwa inu, Sipadzakhala pano mwala umodzi pa unzake, umene sudzagwetsedwa. Ndipo pamene Iye analikukhala pansi pa phiri la Azitona, ophunzira anadza kwa Iye pa yekha, nanena, Mutiuze ife zija zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro cha kufika kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthawi ya pansi pano? Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Yang'anirani, asasokeretse inu munthu. Pakuti ambiri adzafika m'dzina langa, nadzanena, Ine ndine Khristu, nadzasokeretsa anthu ambiri. Koma inu mudzayamba kumva za nkhondo, ndi mbiri za nkhondo; onani, musadere nkhawa; pakuti kuyenera kuti izi zioneke; koma chitsiriziro sichinafike. Pakuti mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zivomezi m'malo akutiakuti. Koma ndizo zonsezi zowawa zoyamba. Pamenepo adzakuperekani kunsautso, nadzakuphani; ndipo anthu a mitundu yonse adzadana nanu, chifukwa cha dzina langa. Ndipo pomwepo ambiri adzakhumudwa, nadzaperekana wina ndi mnzake, nadzadana wina ndi mnzake. Ndipo aneneri onama ambiri adzauka, nadzasokeretsa anthu ambiri. Ndipo chifukwa cha kuchuluka kwa kusaweruzika, chikondano cha anthu aunyinji chidzazilala. Koma iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka. Ndipo Uthenga uwu Wabwino wa Ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro. Chifukwa chake m'mene mukadzaona chonyansa cha kupululutsa, chimene chidanenedwa ndi Daniele mneneri, chitaima m'malo oyera (iye amene awerenga m'kalata azindikire) pomwepo iwo ali m'Yudeya athawire kumapiri: iye ali pamwamba pa chindwi, asatsikire kunyamula za m'nyumba mwake; ndi iye wa m'munda asabwere kutenga chofunda chake. Koma tsoka ali nalo iwo akukhala ndi pakati, ndi akuyamwitsa ana m'masiku awo! Ndipo pempherani kuti kuthawa kwanu kusakhale pa nyengo yachisanu, kapena pa Sabata; pakuti pomwepo padzakhala masauko akulu, monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso. Ndipo akadaleka kufupikitsidwa masiku awo, sakadapulumuka munthu aliyense: koma chifukwa cha osankhidwawo masiku awo adzafupikitsidwa. Pomwepo munthu akanena kwa inu, Onani, Khristu ali kuno, kapena uko musamvomereze; chifukwa Akhristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikulu ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe. Onani ndakuuziranitu pasadafike. Chifukwa chake akanena kwa inu, Onani, Iye ali m'chipululu; musamukeko. Onani, ali m'zipinda; musavomereze. Pakuti monga mphezi idzera kum'mawa, nionekera kufikira kumadzulo; kotero kudzakhalanso kufika kwake kwa Mwana wa Munthu. Kumene kulikonse uli mtembo, miimba idzasonkhanira konko. Koma pomwepo, atapita masauko a masiku awo, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzaonetsa kuwala kwake, ndi nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndi mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka: ndipo pomwepo padzaoneka m'thambo chizindikiro cha Mwana wa Munthu; ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadziguguda pachifuwa, nidzapenya Mwana wa Munthu alinkudza pa mitambo ya kumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu. Ndipo Iye adzatumiza angelo ake ndi kulira kwakukulu kwa lipenga, ndipo iwo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kumphepo zinai, kuyambira malekezero a thambo kufikira malekezero ake ena. Koma phunzirani ndi mkuyu fanizo lake; pamene tsopano nthambi yake ili yanthete, niphuka masamba ake, muzindikira kuti dzinja liyandikira; chomwechonso inu, pamene mudzaona zimenezo, zindikirani kuti Iye ali pafupi, inde pakhomo. Indetu ndinena kwa inu, mbadwo uwu sudzatha kuchoka, kufikira zinthu zonsezi zidzachitidwa. Thambo ndi dziko lapansi zidzachoka, koma mau anga sadzachoka ai. Koma za tsiku ili ndi nthawi yake sadziwa munthu aliyense, angakhale angelo a Kumwamba, kapena Mwana, koma Atate yekha. Ndipo monga masiku a Nowa, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa Munthu. Pakuti monga m'masiku aja, chisanafike chigumula, anthu analinkudya ndi kumwa, analikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa m'chingalawa, Ndipo iwo sanadziwe kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa Munthu. Pomwepo adzakhala awiri m'munda; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa: awiri adzakhala opera pamphero; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa. Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziwa tsiku lake lakufika Ambuye wanu. Koma dziwani ichi, kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yiti mbala ikudza, iye akadadikira, ndipo sakadalola kuti nyumba yake ibooledwe. Chifukwa chake khalani inunso okonzekeratu; chifukwa munthawi m'mene simuganizira, Mwana wa Munthu adzadza. Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake anamkhazika woyang'anira banja lake, kuwapatsa zakudya pa nthawi yake? Wodala kapolo amene mbuye wake, pakufika, adzampeza iye alikuchita chotero. Indetu, ndinena kwa inu, kuti adzamkhazika iye woyang'anira zinthu zake zonse. Koma kapolo woipa akanena mumtima mwake, Mbuye wanga wachedwa; nadzayamba kupanda akapolo anzake, nadya ndi kumwa pamodzi ndi oledzera; mbuye wa kapoloyo adzafika tsiku losamuyembekeza iye, ndi nthawi yosadziwa iye, nadzamdula, nadzaika pokhala pake ndi anthu onyenga; pomwepo padzakhala kulira ndi kukukuta mano. Pomwepo Ufumu wa Kumwamba udzafanizidwa ndi anamwali khumi, amene anatenga nyali zao, natuluka kukakomana ndi mkwati. Ndipo asanu a iwo anali opusa, ndi asanu anali ochenjera. Pakuti opusawo, m'mene anatenga nyali zao, sanadzitengeranso mafuta; koma anzeruwo anatenga mafuta m'nsupa zao, pamodzi ndi nyali zao. Ndipo pamene mkwati anachedwa, onsewo anaodzera, nagona tulo. Koma pakati pa usiku panali kufuula, Onani, mkwati! Tulukani kukakomana naye. Pomwepo anauka anamwali onse amenewo, nakonza nyali zao. Ndipo opusa anati kwa ochenjera, Tipatseniko ena a mafuta anu; chifukwa nyali zathu zilikuzima. Koma ochenjera anayankha nati, Kapena sangakwanire ife ndi inu; koma makamaka mukani kwa ogulitsa malonda, mukadzigulire inu nokha. Ndipo pamene iwo analikumuka kukagula, mkwati anafika; ndipo okonzekawo analowa naye pamodzi muukwati; ndipo anatseka pakhomo. Koma pambuyo pake anadzanso anamwali enawo, nati, Mbuye, Mbuye, mutitsegulire ife. Koma iye anayankha nati, Indetu ndinena kwa inu, sindikudziwani. Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziwa tsiku lake, kapena nthawi yake. Pakuti monga munthu, wakunka ulendo, aitana akapolo ake, napereka kwa iwo chuma chake. Ndipo mmodzi anampatsa ndalama za matalente zisanu, ndi wina ziwiri, ndi wina imodzi; kwa iwo onse monga nzeru zao; namuka iye. Pomwepo uyo amene analandira matalente asanu, anapita kugula nazo malonda, napindulapo matalente ena asanu. Chimodzimodzi uyo wa awiriwo, anapindulapo ena awiri. Koma uyo amene analandira imodziyo anamuka, nakumba pansi, naibisa talente ya mbuye wake. Ndipo itapita nthawi yaikulu, anabwera mbuye wa akapolo awo, nawerengera nao pamodzi. Ndipo uyo amene adalandira matalente asanu anadza, ali nawo matalente ena asanu, nanena, Mbuye, munandipatsa matalente asanu, onani ndapindulapo matalente ena asanu. Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m'chikondwerero cha mbuye wako. Ndipo wa matalente awiriwo anadzanso, nati, Mbuye, munandipatsa ine matalente awiri; onani, ndapindulapo matalente ena awiri. Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m'chikondwerero cha mbuye wako. Ndipo uyonso amene analandira talente imodzi, anadza, nati, Mbuye, ndinakudziwani inu kuti ndinu munthu wouma mtima, wakututa kumene simunafesa, ndi wakusonkhanitsa kumene simunawaza; ndinaopa ine, ndinapita, ndinabisa pansi talente yanu: onani, siyi talente yanuyo. Koma mbuye wake anayankha, nati kwa iye, Kapolo iwe woipa ndi waulesi, unadziwa kuti ndimatuta kumene sindinafesa, ndi kusonkhanitsa kumene sindinawaza; chifukwa chake ukadapereka ndalama zanga kwa okongola ndalama, ndipo ine pobwera ndikadatenga zanga ndi phindu lake. Chifukwa chake chotsani kwa iye ndalamayo, muipatse kwa amene ali nazo ndalama khumi. Pakuti kwa yense amene ali nazo, kudzapatsidwa, ndipo iye adzakhala nazo zochuluka: koma kwa iye amene alibe, kudzachotsedwa, chingakhale chimene anali nacho. Ndipo ponyani kapoloyo wopanda pake kumdima wakunja; kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano. Koma pamene Mwana wa Munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo Iye adzakhala pa chimpando cha kuwala kwake: ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse; ndipo Iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi; nadzakhalitsa nkhosa kudzanja lake lamanja, koma mbuzi kulamanzere. Pomwepo Mfumuyo idzanena kwa iwo a kudzanja lake lamanja, Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, lowani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi: pakuti ndinali ndi njala, ndipo munandipatsa Ine kudya; ndinali ndi ludzu, ndipo munandimwetsa Ine; ndinali mlendo, ndipo munachereza Ine; wamaliseche Ine, ndipo munandiveka; ndinadwala, ndipo munadza kucheza ndi Ine; ndinali m'nyumba yandende, ndipo munadza kwa Ine. Pomwepo olungama adzamyankha Iye kuti, Ambuye, tinakuonani Inu liti wanjala, ndi kukudyetsani? Kapena waludzu, ndi kukumwetsani? Ndipo tinaona Inu liti mlendo, ndi kukucherezani? Kapena wamaliseche, ndi kukuvekani? Ndipo tinakuonani Inu liti wodwala, kapena m'nyumba yandende, ndipo tinadza kwa Inu? Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang'onong'ono awa, munandichitira ichi Ine. Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a kudzanja lamanzere, Chokani kwa Ine otembereredwa inu, kumoto wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi angelo ake: pakuti ndinali ndi njala, ndipo simunandipatsa Ine kudya: ndinali ndi ludzu, ndipo simunandimwetsa Ine: ndinali mlendo, ndipo simunandilandira Ine; wamaliseche ndipo simunandiveka Ine; wodwala, ndi m'nyumba yandende, ndipo simunadza kundiona Ine. Pomwepo iwonso adzayankha kuti, Ambuye, tinakuonani liti wanjala, kapena waludzu, kapena mlendo, kapena wamaliseche, kapena m'nyumba yandende, ndipo ife sitinakutumikirani Inu? Pomwepo Iye adzayankha iwo kuti, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munalibe kuchitira ichi mmodzi wa awa ang'onong'ono, munalibe kundichitira ichi Ine. Ndipo amenewa adzachoka kunka ku chilango cha nthawi zonse; koma olungama kumoyo wa nthawi zonse. Ndipo panali pamene Yesu anatha mau onse amenewa, anati kwa ophunzira ake, Mudziwa kuti akapita masiku awiri, Paska afika, ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kupachikidwa pamtanda. Pomwepo anasonkhana ansembe aakulu, ndi akulu a anthu, kubwalo la mkulu wa ansembe, dzina lake Kayafa; nakhala upo wakuti amgwire Yesu ndi chinyengo, namuphe. Koma ananena iwo, pa nthawi la chikondwerero iai, kuti pasakhale phokoso la anthu. Ndipo pamene Yesu anali m'Betaniya, m'nyumba ya Simoni wakhate, anadza kwa Iye mkazi, anali nayo nsupa ya alabastero ndi mafuta onunkhira bwino a mtengo wapatali, nawatsanulira pamutu pake, m'mene Iye analikukhala pachakudya. Koma m'mene ophunzira anaona, anada mtima, nanena, Chifukwa ninji kuononga kumeneku? Pakuti mafuta awa akadagulitsa ndalama zambiri, ndi kuzipatsa anthu aumphawi. Koma Yesu podziwa, anati kwa iwo, Mumvutiranji mkaziyu? Popeza andichitira Ine ntchito yabwino. Pakuti nthawi zonse muli nao aumphawi pamodzi nanu; koma simuli ndi Ine nthawi zonse. Pakuti mkaziyo, m'mene anathira mafuta awa pathupi panga, wandichitiratu ichi pa kuikidwa kwanga. Indetu ndinena kwa inu, kumene kulikonse Uthenga uwu Wabwino udzalalikidwa m'dziko lonse lapansi, ichi chimene mkaziyo anachitachi chidzakambidwanso chikumbukiro chake. Pomwepo mmodzi wa khumi ndi awiriwo, dzina lake Yudasi Iskariote, anamuka kwa ansembe aakulu, nati, Mufuna kundipatsa chiyani, ndipo ine ndidzampereka Iye kwa inu? Ndipo iwo anamwerengera iye ndalama zasiliva makumi atatu. Ndipo kuyambira pamenepo iye anafunafuna nthawi yabwino yakuti ampereke Iye. Ndipo tsiku loyamba la mkate wopanda chotupitsa, ophunzira anadza kwa Yesu, nati, Mufuna tikakonzere kuti Paska, kuti mukadye? Nati Iye, Mukani kumzinda kwa munthu wangana, mukati kwa Iye, Mphunzitsi anena, Nthawi yanga yayandikira; ndidzadya Paska kwanu pamodzi ndi ophunzira anga. Ndipo ophunzira anachita monga Yesu anawauza, nakonza Paska. Ndipo pakufika madzulo, Iye analinkukhala pachakudya pamodzi ndi ophunzira khumi ndi awiri; ndipo m'mene analinkudya, Iye anati, Indetu ndinena kwa inu, mmodzi wa inu adzandipereka Ine. Ndipo iwo anagwidwa ndi chisoni chachikulu, nayamba kunena kwa Iye mmodzimmodzi, Kodi ndine, Ambuye? Ndipo Iye anayankha nati, Iye amene asunsa pamodzi ndi Ine dzanja lake m'mbale, yemweyu adzandipereka Ine. Mwana wa Munthu achokatu, monga kunalembedwa za Iye; koma tsoka ali nalo munthu amene Mwana wa Munthu aperekedwa ndi iye! Kukadakhala bwino kwa munthuyo ngati sakadabadwa. Ndipo Yudasi, womperekayo anayankha nati, Kodi ndine, Rabi? Iye ananena kwa iye, Iwe watero. Ndipo pamene iwo analinkudya, Yesu anatenga mkate, nadalitsa, naunyema; ndipo m'mene anapatsa kwa ophunzira, anati, Tengani, idyani; ichi ndi thupi langa. Ndipo pamene anatenga chikho, anayamika, napatsa iwo, nanena, Mumwere ichi inu nonse, pakuti ichi ndi mwazi wanga wa pangano wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri ku kuchotsa machimo. Ndipo ndinena kwa inu, sindidzamwanso chipatso ichi champesa, kufikira tsiku limene ndidzamwa chatsopano, pamodzi ndi inu, mu Ufumu wa Atate wanga. Ndipo pamene anaimba nyimbo, anatuluka kunka kuphiri la Azitona. Pamenepo Yesu ananena kwa iwo, Inu nonse mudzakhumudwa chifukwa cha Ine usiku uno; pakuti kwalembedwa, Ndidzakantha mbusa, ndipo zidzabalalika nkhosa za gulu. Koma nditauka ndidzatsogolera inu ku Galileya. Koma Petro ananena kwa Iye, Ngakhale onse adzakhumudwa chifukwa cha Inu, ine sindidzakhumudwa nthawi zonse. Yesu anati kwa iye, Indetu ndinena kwa iwe, kuti usiku uno, tambala asanalire, udzandikana Ine katatu. Petro ananena kwa Iye, Ngakhale ine ndikafa ndi Inu, sindidzakukanani Inu iai. Anateronso ophunzira onse. Pomwepo Yesu anadza ndi iwo kumalo otchedwa Getsemani, nanena kwa ophunzira ake, Bakhalani inu pompano, ndipite uko ndikapemphere. Ndipo anatenga Petro ndi ana awiri a Zebedeo pamodzi naye, nayamba kugwidwa ndi chisoni ndi kuthedwa nzeru. Pamenepo ananena kwa iwo, Moyo wanga uli wozingidwa ndi chisoni cha kufika nacho kuimfa; khalani pano muchezere pamodzi ndi Ine. Ndipo anamuka patsogolo pang'ono, nagwa nkhope yake pansi, napemphera, nati, Atate ngati nkutheka, chikho ichi chindipitirire Ine; koma si monga ndifuna Ine, koma Inu. Ndipo anadza kwa ophunzira, nawapeza iwo ali m'tulo, nanena kwa Petro, Nkutero kodi? Simukhoza kuchezera ndi Ine mphindi imodzi? Chezerani ndi kupemphera, kuti mungalowe m'kuyesedwa: mzimutu uli wakufuna, koma thupi lili lolefuka. Anamukanso kachiwiri, napemphera, nati, Atate wanga, ngati ichi sichingandipitirire, koma ndimwere ichi, kufuna kwanu kuchitidwe. Ndipo anabweranso, nawapeza iwo ali m'tulo, pakuti zikope zao zinalemera ndi tulo. Ndipo anawasiyanso, napemphera kachitatu, nateronso mau omwewo. Pomwepo anadza kwa ophunzira, nanena kwa iwo, Gonani nthawi yatsalayi, mupumule; onani, nthawi yafika, ndipo Mwana wa Munthu aperekedwa m'manja a ochimwa. Ukani, timuke; taonani, iye wakundipereka wayandikira. Ndipo Iye ali chilankhulire, onani, Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anadza, ndi pamodzi ndi iye khamu lalikulu la anthu, ndi malupanga ndi mikunkhu, kuchokera kwa ansembe aakulu ndi akulu a anthu. Koma wompereka Iye anawapatsa chizindikiro, nanena, Iye amene ndidzampsompsona ndiyeyo, mumgwire Iye. Ndipo pomwepo anadza kwa Yesu, nati, Tikuoneni, Rabi; nampsompsonetsa. Ndipo Yesu anati kwa iye, Mnzanga, wafikiranji iwe? Pomwepo iwo anadza, namthira Yesu manja, namgwira Iye. Ndipo onani, mmodzi wa iwo anali pamodzi ndi Yesu, anatansa dzanja lake, nasolola lupanga lake, nakantha kapolo wa mkulu wa ansembe, nadula khutu lake. Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Tabweza lupanga lako m'chimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzaonongeka ndi lupanga. Kapena uganiza kuti sindingathe kupemphera Atate wanga, ndipo Iye adzanditumizira tsopano lino mabungwe a angelo oposa khumi ndi awiri? Koma pakutero malembo adzakwaniridwa bwanji, pakuti kuyenera chomwecho? Nthawi yomweyo Yesu anati kwa makamuwo a anthu, Kodi munatulukira kundigwira Ine ndi malupanga ndi mikunkhu, ngati wachifwamba? Tsiku ndi tsiku ndimakhala m'Kachisi kuphunzitsa, ndipo simunandigwira. Koma izi zonse zinachitidwa, kuti zolembedwa za aneneri zikwaniridwe. Pomwepo ophunzira onse anamsiya Iye, nathawa. Ndipo iwo akugwira Yesu ananka naye kwa Kayafa, mkulu wa ansembe, kumene adasonkhana alembi ndi akulu omwe. Koma Petro anamtsata kutali, kufikira kubwalo la mkulu wa ansembe, nalowamo, nakhala pansi ndi anyamata, kuti aone chimaliziro. Ndipo ansembe aakulu ndi akulu a milandu onse anafunafuna umboni wonama wakutsutsa Yesu, kuti amuphe Iye; koma sanaupeze zingakhale mboni zonama zambiri zinadza. Koma pambuyo pake anadza awiri, nati, Uyu ananena kuti, Ndikhoza kupasula Kachisi wa Mulunguyu, ndi kummanganso masiku atatu. Ndipo mkulu wa ansembe anaimirira, nati kwa Iye, Suvomera kanthu kodi? Nchiyani ichi chimene awa akunenera Iwe? Koma Yesu anangokhala chete. Ndipo mkulu wa ansembe ananena kwa Iye, Ndikulumbiritsa Iwe pa Mulungu wamoyo, kuti utiuze ife ngati Iwe ndiwe Khristu, Mwana wa Mulungu. Yesu anati kwa iye, Mwatero, koma ndinenanso kwa inu, Kuyambira tsopano mudzaona Mwana wa Munthu ali kukhala kudzanja lamanja la mphamvu, ndi kufika pa mitambo ya kumwamba. Pomwepo mkulu wa ansembe anang'amba zovala zake, nati, Achitira Mulungu mwano; tifuniranji mboni zina? Onani, tsopano mwamva mwanowo; muganiza bwanji? Iwo anayankha nati, Ali woyenera kumupha. Pomwepo iwo anathira malovu pankhope pake, nambwanyula Iye; ndipo ena anampanda khofu, nati, Utilote ife, Khristu Iwe; wakumenya Iwe ndani? Ndipo Petro adakhala pabwalo: ndipo mdzakazi anadza kwa iye, nanena, Iwenso unali ndi Yesu wa ku Galileya. Koma iye anakana pamaso pa anthu onse, kuti, Chimene unena sindichidziwa. Ndipo pamene iye anatuluka kunka kuchipata, mkazi wina anamuona, nati kwa iwo a pomwepo, Uyonso anali ndi Yesu Mnazarayo. Ndipo anakananso ndi chilumbiro, kuti, Sindidziwa munthuyo. Ndipo popita nthawi yaing'ono, iwo akuimapo anadza, nati kwa Petro, Zoonadi, iwenso uli wa iwo; pakuti malankhulidwe ako akuzindikiritsa iwe. Pamenepo iye anayamba kutemberera ndi kulumbira, kuti, Sindidziwa munthuyo. Ndipo pompo tambala analira. Ndipo Petro anakumbukira mau amene Yesu adati, Asanalire tambala udzandikana katatu. Ndipo anatulukira kunja, nalira ndi kuwawa mtima. Ndipo pakudza mamawa, ansembe aakulu ndi akulu a anthu onse anakhala upo wakumchitira Yesu, kuti amuphe; ndipo anammanga Iye, namuka naye, nampereka Iye kwa Pilato kazembeyo. Pamenepo Yudasi yemwe anampereka Iye, poona kuti Iye anatsutsidwa kuti afe, analapa, nabweza ndalama zija zasiliva makumi atatu kwa ansembe aakulu ndi akulu, nanena, Ndinachita koipa ine, pakupereka mwazi wosalakwa. Koma iwo anati, Tili nacho chiyani ife? Udzionere wekha. Ndipo iye anataya pansi ndalamazo pa Kachisi, nachokapo, nadzipachika yekha pakhosi. Ndipo ansembe aakulu anatenga ndalamazo, nati, Sikuloledwa kuziika m'chosonkhera ndalama za Mulungu, chifukwa ndizo mtengo wa mwazi. Koma anapangana, nazigula munda wa woumba mbiya, ukhale manda a alendo. Chifukwa chake munda umenewu anautcha, Munda-wa-mwazi, kufikira lero lino. Pamenepo chinakwaniridwa chonenedwa ndi Yeremiya mneneri, ndi kuti, Ndipo iwo anatenga ndalamazo zasiliva makumi atatu, mtengo wa uja wowerengedwa mtengo wake, amene iwo a ana a Israele anawerenga mtengo wake; ndipo anazipereka kugula munda wa woumba mbiya, monga anandilamulira ine Ambuye. Ndipo Yesu anaimirira pamaso pa kazembe, ndipo kazembeyo anamfunsa Iye kuti, Kodi Iwe ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo Yesu anati kwa iye, Mwatero. Ndipo pakumnenera Iye ansembe aakulu ndi akulu, Iye sanayankhe kanthu. Pomwepo Pilato ananena kwa Iye, Sukumva kodi zinthu zambiri zotere akunenera Iwe? Ndipo sanayankhe Iye, ngakhale mau amodzi, kotero kuti kazembe anazizwa ndithu. Ndipo pa chikondwerero kazembe adazolowera kumasulira anthu mmodzi wandende, amene iwo anafuna. Ndipo pa nthawi yomweyo anali ndi wandende wodziwika, dzina lake Barabasi. Chifukwa chake pamene anasonkhana, Pilato ananena kwa iwo, Mufuna kuti ndikumasulireni yani? Barabasi kodi, kapena Yesu, wotchedwa Khristu? Pakuti anadziwa kuti anampereka Iye mwanjiru. Ndipo pamene Pilato analikukhala pa mpando wakuweruza, mkazi wake anatumiza mau kwa iye, kunena, Musachite kanthu ndi munthu wolungamayo; pakuti lero m'kulota ine ndasauka kwambiri chifukwa cha Iye. Koma ansembe aakulu ndi akulu anapangira anthu kuti apemphe Barabasi, koma kuti aononge Yesu. Koma kazembe anati kwa iwo, Mufuna kuti ndikumasulireni uti wa awa awiri? Ndipo iwo anati, Barabasi. Pilato ananena kwa iwo, Nanga ndidzachita chiyani ndi Yesu, wotchedwa Khristu? Onse anati, Apachikidwe pamtanda. Ndipo iye anati, Chifukwa ninji? Anachita choipa chotani? Koma iwo anafuulitsa kopambana, Apachikidwe pamtanda. Koma Pilato poona kuti sanafitse, koma kuti linapambana phokoso, anatenga madzi, nasamba manja pamaso pa khamulo, nati, Ine ndilibe kuchimwira mwazi wa munthu uyu wolungama, mudzionere nokha. Ndipo anthu onse anavomereza, ndi kuti, Mwazi wake uli pa ife ndi pa ana athu. Pomwepo iye anamasulira iwo Barabasi, koma anakwapula Yesu, nampereka Iye kuti akampachike pamtanda. Pomwepo asilikali a kazembe anamuka naye Yesu kubwalo la milandu, nasonkhanitsa kwa Iye khamu lao lonse. Ndipo anavula malaya ake, namveka malaya ofiira achifumu. Ndipo analuka korona waminga, namveka pamutu pake, namgwiritsa bango m'dzanja lamanja lake; ndipo anagwada pansi pamaso pake, namchitira chipongwe, nati, Tikuoneni, mfumu ya Ayuda! Namthira malovu, natenga bango, nampanda Iye pamutu. Ndipo pamene anatha kumchitira Iye chipongwe, anavula malaya aja, namveka Iye malaya ake, natsogoza Iye kukampachika pamtanda. Ndipo pakutuluka pao anapeza munthu wa ku Kirene, dzina lake Simoni, namkakamiza iye kuti anyamule mtanda wake. Ndipo pamene anadza kumalo dzina lake Gologota, ndiko kunena kuti, Malo a Bade, anamwetsa Iye vinyo wosanganiza ndi ndulu; ndipo Iye, m'mene analawa, sanafune kumwa. Ndipo pamene anampachika Iye, anagawana zovala zake ndi kulota maere: nakhala iwo pansi, namdikira kumeneko. Ndipo anaika pamwamba pamutu pake mlandu wake wolembedwa: UYU NDI YESU MFUMU YA AYUDA. Pamenepo anapachika pamodzi ndi Iye achifwamba awiri, mmodzi kudzanja lamanja, ndi wina kulamanzere. Ndipo anthu akupitirirapo anamchitira mwano Iye ndi kupukusa mitu yao, nati, Nanga Iwe, wopasula Kachisi, ndi kummanganso masiku atatu, tadzipulumutsa wekha; ngati uli Mwana wa Mulungu, tatsika pamtandapo. Chomwechonso ansembe aakulu, pamodzi ndi alembi ndi akulu anamchitira chipongwe, nati, Anapulumutsa ena, sangathe kudzipulumutsa yekha. Ndiye mfumu ya Aisraele; atsike tsopano pamtandapo, ndipo tidzamkhulupirira Iye. Amakhulupirira Mulungu; Iye ampulumutse tsopano, ngati amfuna; pakuti anati, Ine ndine Mwana wa Mulungu. Ndiponso achifwambawo opachikidwa pamodzi ndi Iye, anamlalatira Iye mau amodzimodzi. Ndipo ora lachisanu ndi chimodzi panali mdima pa dziko lonse, kufikira ora lachisanu ndi chinai. Ndipo poyandikira ora lachisanu ndi chinai, Yesu anafuula ndi mau akulu, kunena, Eli, Eli, lama sabakitani? ndiko kunena kuti, Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine? Ndipo ena a iwo akuimirira komweko, pamene anamva, ananena, Uyo aitana Eliya. Ndipo pomwepa mmodzi wa iwo anathamanga, natenga chinkhupule, nachidzaza ndi vinyo wosasa, nachiika pabango, namwetsa Iye. Koma ena anati, Taleka, tione ngati Eliya adzafika kudzampulumutsa. Ndipo Yesu, pamene anafuula ndi mau akulu, anapereka mzimu wake. Ndipo onani, chinsalu chotchinga cha m'Kachisi chinang'ambika pakati, kuchokera kumwamba kufikira pansi; ndipo dziko linagwedezeka, ndi miyala inang'ambika; ndi manda anatseguka, ndi mitembo yambiri ya anthu oyera mtima, akugona kale, inauka; ndipo anatuluka m'manda mwao pambuyo pa kuuka kwake, nalowa m'mzinda woyera, naonekera kwa anthu ambiri. Ndipo anali naye akudikira Yesu, anaona chivomezi, ndi zinthu zimene zinachitidwa, anaopa kwambiri, nanena, Indedi Uyu ndiye Mwana wa Mulungu. Ndipo anali pomwepo akazi ambiri, akuyang'anira patali, omwe anatsata Yesu kuchokera ku Galileya, namatumikira Iye; mwa iwo amene munali Maria wa Magadala, ndi Maria amake wa Yakobo, ndi wa Yosefe, ndi amake wa ana a Zebedeo. Ndipo pamene panali madzulo, anadza munthu wachuma wa ku Arimatea, dzina lake Yosefe, amene analinso wophunzira wa Yesu; yemweyo anapita kwa Pilato, napempha mtembo wa Yesu. Pomwepo Pilato analamula kuti uperekedwe. Ndipo Yosefe anatenga mtembo, naukulunga m'nsalu yabafuta yoyeretsa, nauika m'manda ake atsopano, osemedwa m'mwala, nakunkhunizira mwala waukulu pakhomo pa manda, nachokapo. Ndipo Maria wa Magadala anali pamenepo, ndi Maria winayo, anakhala pansi popenyana ndi mandawo. Ndipo m'mawa mwake, ndilo dzuwa lotsatana ndi tsiku lokonzera, ansembe aakulu ndi Afarisi anasonkhanira kwa Pilato, nanena, Mfumu, takumbukira ife kuti wonyenga uja anati, pamene anali ndi moyo, Ndidzauka pofika masiku atatu. Chifukwa chake mulamule kuti asindikize pamandapo, kufikira tsiku lachitatulo, kuti kapena ophunzira ake angadze, nadzamuba Iye, nadzanena kwa anthu, kuti Iye anauka kwa akufa: ndipo chinyengo chomaliza chidzaposa choyambacho. Pilato anati kwa iwo, Tengani alonda; mukani, kasungeni monga mudziwa. Ndipo iwo anamuka, nasunga manda, nasindikizapo chizindikiro pamwalapo, iwo pamodzi ndi alondawo. Ndipo popita tsiku la Sabata, mbandakucha, tsiku lakuyamba la sabata, anadza Maria wa Magadala, ndi Maria winayo, kudzaona manda. Ndipo onani, panali chivomezi chachikulu; pakuti mngelo wa Ambuye anatsika Kumwamba, nafika kukunkhuniza mwalawo, nakhala pamwamba pake. Kuonekera kwake kunali ngati mphezi, ndi chovala chake choyeretsa ngati matalala; ndipo ndi kuopsa kwake alondawo ananthunthumira, nakhala ngati anthu akufa. Koma mngelo anayankha, nati kwa akaziwo, Musaope inu; pakuti ndidziwa inu mulikufuna Yesu, amene anapachikidwa. Iye mulibe muno iai; pakuti anauka, monga ananena. Idzani muno mudzaone malo m'mene anagonamo Ambuye. Ndipo pitani msanga, muuze ophunzira ake, kuti, Wauka kwa akufa; ndipo onani, akutsogolerani ku Galileya; mudzamuona Iye komweko; onani, ndakuuzani inu. Ndipo iwo anachoka msanga kumanda, ndi mantha ndi kukondwera kwakukulu, nathamanga kukauza ophunzira ake. Ndipo onani, Yesu anakomana nao, nanena, Tikuoneni. Ndipo iwo anadza, namgwira Iye mapazi ake, namgwadira. Pomwepo Yesu ananena kwa iwo, Musaope; pitani, kauzeni abale anga kuti amuke ku Galileya, ndipo adzandiona Ine kumeneko. Ndipo pamene iwo analikupita, onani, ena a alonda anafika kumzinda, nauza ansembe aakulu zonse zimene zinachitidwa. Ndipo pamene anasonkhana pamodzi ndi akulu, anakhala upo, napatsa asilikaliwo ndalama zambiri, nati, Kazinenani, kuti ophunzira ake anadza usiku, namuba Uja m'mene ife tinali m'tulo. Ndipo ngati ichi chidzamveka kwa kazembe, ife tidzamgwetsa mtima, ndipo tidzakukhalitsani opanda nkhawa. Ndipo iwo analandira ndalamazo, nachita monga anawalangiza: ndipo mbiri iyo inabuka mwa Ayuda, kufikira lero lomwe. Koma ophunzira khumi ndi mmodziwo anamuka ku Galileya, kuphiri kumene Yesu anawapangira. Ndipo pamene anamuona Iye, anamlambira; koma ena anakayika. Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pa dziko lapansi. Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano. Chiyambi chake cha Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu. Monga mwalembedwa m'Yesaya mneneri, Ona, ndituma mthenga wanga patsogolo pa nkhope yanu, amene adzakonza njira yanu. Mau a wofuula m'chipululu, konzani khwalala la Ambuye, lungamitsani njira zake. Yohane anadza nabatiza m'chipululu, nalalikira ubatizo wa kutembenuka mtima wakuloza ku chikhululukiro cha machimo. Ndipo anatuluka a ku dziko lonse la Yudeya, ndi a ku Yerusalemu onse; nadza kwa iye nabatizidwa ndi iye mumtsinje Yordani, powulula machimo ao. Ndipo Yohane anavala ubweya wa ngamira, ndi lamba lachikopa m'chuuno mwake, nadya dzombe ndi uchi wa kuthengo. Ndipo analalikira, kuti, Wondipambana ine mphamvu akudza pambuyo panga, sindiyenera kuwerama kumasula lamba la nsapato zake ine. Ndakubatizani inu ndi madzi; koma Iye adzakubatizani ndi Mzimu Woyera. Ndipo kunali masiku omwewo, Yesu anadza kuchokera ku Nazarete wa ku Galileya, nabatizidwa ndi Yohane m'Yordani. Ndipo pomwepo, alimkukwera potuluka m'madzi, anaona Iye thambo litang'ambika, ndi Mzimu alikutsikira pa Iye monga nkhunda: ndipo mau anatuluka m'thambo, Mwana wanga wokondedwa ndiwe, mwa Iwe ndikondwera bwino. Ndipo pomwepo Mzimu anamkakamiza kunka kuchipululu. Ndipo anakhala m'chipululu masiku makumi anai woyesedwa ndi Satana; nakhala ndi zilombo, ndipo angelo anamtumikira. Ndipo ataperekedwa Yohane, Yesu anadza ku Galileya, nalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, nanena, Nthawi yakwanira, ndipo Ufumu wa Mulungu wayandikira; tembenukani mtima, khulupirirani Uthenga Wabwino. Ndipo pakuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi Andrea, mbale wake wa Simoni, alinkuponya khoka m'nyanja; pakuti anali asodzi. Ndipo Yesu ananena nao, Idzani pambuyo panga, ndipo ndidzakusandutsani inu asodzi a anthu. Ndipo pomwepo anasiya makoka ao, namtsata Iye. Ndipo atapita patsogolo pang'ono, anaona Yakobo, mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake, iwonso anali m'chombo nakonza makoka ao. Ndipo pomwepo anawaitana: ndipo anasiya atate wao Zebedeo m'chombomo pamodzi ndi antchito olembedwa, namtsata. Ndipo iwo analowa m'Kapernao; ndipo pomwepo pa tsiku la Sabata iye analowa m'sunagoge naphunzitsa. Ndipo anazizwa ndi chiphunzitso chake; pakuti anaphunzitsa monga mwini mphamvu, si monga alembi. Ndipo pomwepo panali munthu m'sunagoge mwao ali ndi mzimu wonyansa; ndipo anafuula iye. Kuti, Tili ndi chiyani ife ndi Inu Yesu wa ku Nazarete? Kodi mwadza kudzationonga ife: Ndikudziwani, ndinu Woyerayo wa Mulungu. Ndipo Yesu anaudzudzula, kuti, Khala uli chete, nutuluke mwa iye. Ndipo mzimu wonyansa, pomng'amba, ndi kufuula ndi mau akulu, unatuluka mwa iye. Ndipo anazizwa onse, kotero kuti anafunsana mwa iwo okha, kuti, Ichi nchiyani? Chiphunzitso chatsopano! Ndi mphamvu alamula ingakhale mizimu yonyansa, ndipo imvera Iye. Ndipo mbiri yake inabuka pompaja kudziko lonse la Galileya lozungulirapo. Ndipo pomwepo, potuluka m'sunagoge, iwo analowa m'nyumba ya Simoni ndi Andrea pamodzi ndi Yakobo ndi Yohane. Ndipo mpongozi wake wa Simoni anali gone wodwala malungo; ndipo pomwepo anamuuza za iye: ndipo anadza namgwira dzanja, namuutsa; ndipo malungo anamleka, ndipo anawatumikira iwo. Ndipo madzulo, litalowa dzuwa, anadza nao kwa Iye onse akudwala, ndi akugwidwa ndi ziwanda. Ndipo mudzi wonse unasonkhana pakhomo. Ndipo anachiritsa anthu ambiri akudwala nthenda za mitundumitundu, natulutsa ziwanda zambiri; ndipo sanalole ziwandazo zilankhule, chifukwa zinamdziwa Iye. Ndipo m'mawa mwake anauka usikusiku, natuluka namuka kuchipululu, napemphera kumeneko. Ndipo Simoni ndi anzake anali naye anamtsata, nampeza, nanena naye, Akufunani Inu anthu onse. Ndipo ananena nao, Tiyeni kwina, kumidzi ili pafupi apa, kuti ndilalikire komwekonso; pakuti ndadzera ntchito imene. Ndipo analowa m'masunagoge mwao m'Galileya monse, nalalikira, natulutsa ziwanda. Ndipo anadza kwa Iye wodwala khate, nampempha Iye, namgwadira, ndi kunena ndi Iye, Ngati mufuna mukhoza kundikonza. Ndipo Yesu anagwidwa chifundo, natansa dzanja namkhudza iye, nanena naye, Ndifuna; khala wokonzedwa. Ndipo pomwepo khate linamchoka, ndipo anakonzedwa. Ndipo anamuuzitsa, namtulutsa pomwepo, nanena naye, Ona, usati unene kanthu kwa munthu aliyense: koma muka, ukadzionetse kwa wansembe, nupereke pa makonzedwe ako zimene adalamulira Mose, zikhale mboni kwa iwo. Koma iye anatuluka nayamba kulalikira ndithu, ndi kubukitsa mauwo, kotero kuti Yesu sanadziwa kulowanso poyera m'mudzi, koma anakhala padera m'mapululu; ndipo anadza kwa Iye anthu a kumalo onse. Ndipo polowanso Iye m'Kapernao atapita masiku ena, kunamveka kuti ali m'nyumba. Ndipo ambiri anaunjikana, kotero kuti anasowa malo, ngakhale pakhomo pomwe; ndipo analankhula nao mau. Ndipo anadza kwa Iye otenga munthu wodwala manjenje, wonyamulidwa ndi anthu anai. Ndipo pamene sanakhoze kufika kuli Iye, chifukwa cha khamu la anthu, anasasula chindwi pokhala Iye; ndipo pamene anatha kuliboola, anatsitsa mphasa m'mene alinkugonamo wodwala manjenjeyo. Ndipo Yesu pakuona chikhulupiriro chao ananena ndi wodwala manjenje, Mwana, machimo ako akhululukidwa. Koma anakhalapo ena a alembi akuganizira mumtima mwao, Munthu amene atero bwanji? Achita mwano; akhoza ndani kukhululukira machimo, koma mmodzi, ndiye Mulungu? Ndipo pomwepo Yesu pozindikira mumtima mwake kuti alikuganizira chomwecho mwa iwo okha, ananena nao, Muganiza bwanji zinthu izi m'mitima yanu? Chapafupi nchiti, kuuza wodwala manjenje kuti, Machimo ako akhululukidwa; kapena kuti, Nyamuka, senza mphasa yako, nuyende? Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali mwini ulamuliro wakukhululukira machimo pa dziko lapansi (ananena ndi wodwala manjenje), Ndikuuza iwe, Nyamuka, senza mphasa yako, numuke kwanu. Ndipo ananyamuka iye pomwepo, nasenza mphasa, natuluka pamaso pa iwo onse; kotero kuti anadabwa onse, nalemekeza Mulungu, nanena kuti, Zotere sitinaziona ndi kale lonse. Ndipo anatulukanso kunka m'mbali mwa nyanja; ndipo linadza kwa Iye khamu lonse la anthu, ndipo anawaphunzitsa. Ndipo pakumuka, naona Levi mwana wa Alifeyo alikukhala polandirira msonkho, ndipo ananena naye, Tsata Ine. Ndipo ananyamuka namtsata Iye. Ndipo kunali kuti anakhala pakudya m'nyumba mwake, ndipo amisonkho ndi ochimwa ambiri anakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake, pakuti anali ambiri, ndipo anamtsata Iye. Ndipo alembi a kwa Afarisi, pakuona kuti alinkudya nao ochimwa ndi amisonkho, ananena ndi ophunzira ake, Uyu akudya ndi kumwa nao amisonkho ndi ochimwa. Ndipo pamene Yesu anamva ichi, ananena nao, Akulimba safuna sing'anga, koma odwala ndiwo; sindinadza kudzaitana olungama, koma ochimwa. Ndipo ophunzira a Yohane ndi Afarisi analinkusala kudya; ndipo anadza, nanena ndi Iye, Bwanji asala kudya ophunzira a Yohane, ndi ophunzira a Afarisi, koma ophunzira anu sasala kudya? Ndipo Yesu ananena nao, Kodi akhoza kusala kudya anyamata a ukwati pamene mkwati ali pamodzi nao? Pokhala ali naye mkwati pamodzi ndi iwo sakhoza kusala. Koma adzadza masiku, pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo pamenepo adzasala kudya tsiku lomwelo. Palibe munthu asokerera chigamba cha nsalu yaiwisi pa chofunda chakale; pena chimene choti chidzakonza chizomolapo, chatsopanocho chizomoka pa chakalecho, ndipo chiboo chikulapo. Ndipo palibe munthu amatsanulira vinyo watsopano m'matumba akale: pena vinyo adzaphulitsa matumba, ndipo aonongeka vinyo, ndi matumba omwe: koma vinyo watsopano amatsanulira m'matumba atsopano. Ndipo kunali kuti anapita Iye pakati pa minda tsiku la Sabata; ndipo ophunzira ake poyenda anayamba kubudula ngala za dzinthu. Ndipo Afarisi ananena ndi Iye, Taona, achitiranji chosaloleka kuchitika tsiku la Sabata? Ndipo ananena nao, Simunawerenga konse chimene anachichita Davide, pamene adasowa, namva njala, iye ndi iwo amene anali pamodzi naye? Kuti analowa m'nyumba ya Mulungu masiku a Abiyatara, mkulu wa ansembe, ndipo anadya mikate yoonetsera, yosaloleka kudya ena, koma ansembe okha, ndipo anawapatsanso iwo amene anali naye? Ndipo ananena nao, Sabata linaikidwa chifukwa cha munthu, si munthu chifukwa cha Sabata; motero Mwana wa Munthu ali mwini tsiku la Sabata lomwe. Ndipo analowanso m'sunagoge; ndipo munali munthu m'menemo ali ndi dzanja lake lopuwala. Ndipo anamuyang'anira Iye, ngati adzamchiritsa tsiku la Sabata; kuti ammange mlandu. Ndipo ananena ndi munthu ali ndi dzanja lopuwala, Taimirira pakati. Ndipo ananena kwa iwo, Kodi nkuloledwa tsiku la Sabata kuchita zabwino, kapena zoipa? Kupulumutsa moyo kapena kupha? Koma anakhala chete. Ndipo m'mene anawaunguza ndi mkwiyo, ndi kumva chisoni chifukwa cha kuuma kwa mitima yao, ananena kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo analitambasula; ndipo linachira dzanja lake. Ndipo Afarisi anatuluka, ndipo pomwepo anamkhalira upo ndi Aherode, wakumuononga Iye. Ndipo Yesu anachokako pamodzi ndi ophunzira ake nanka kunyanja: ndipo linamtsata khamu lalikulu la a ku Galileya, ndi a ku Yudeya, ndi a ku Yerusalemu, ndi a ku Idumeya, ndi a ku tsidya lina la Yordani, ndi a kufupi ku Tiro ndi Sidoni, khamu lalikulu, pakumva zazikuluzo anazichita, linadza kwa Iye. Ndipo anati kwa ophunzira ake, kuti kangalawa kamlinde Iye, chifukwa cha khamulo, kuti angamkanikize Iye, pakuti adawachiritsa ambiri; kotero kuti onse akukhala nazo zowawa anakanikiza Iye, kuti akamkhudze. Ndipo mizimu yonyansa, m'mene inamuona Iye, inamgwadira, nifuula, niti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu. Ndipo anailimbitsira mau kuti isamuulule Iye. Ndipo anakwera m'phiri, nadziitanira iwo amene anawafuna Iye mwini; ndipo anadza kwa Iye. Ndipo anaika khumi ndi awiri, kuti akhale ndi Iye, ndi kuti akawatume kulalikira, ndi kuti akhale nao ulamuliro wakutulutsa ziwanda. Ndipo Simoni anamutcha Petro; ndi Yakobo mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake wa Yakobo, iwo anawatcha Boaneje, ndiko kuti, Ana a bingu; ndi Andrea, ndi Filipo, ndi Bartolomeo, ndi Mateyu, ndi Tomasi, ndi Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo, ndi Simoni Mkanani, ndi Yudasi Iskariote, ndiye amene anampereka Iye. Ndipo anthu ambiri anasonkhananso, kotero kuti sanathe iwo konse kudya. Ndipo pamene abale ake anamva, anadza kudzamgwira Iye; pakuti anati adayaluka. Ndipo alembi amene adatsika ku Yerusalemu ananena kuti, Ali naye Belezebulu, ndipo, Ndi mkulu wao wa ziwanda atulutsa ziwanda. Ndipo m'mene adawaitana iwo, ananena nao m'mafanizo, Satana angathe bwanji kutulutsa Satana? Ndipo ufumu ukagawanika pa uwu wokha, sukhoza kukhazikika. Ndipo nyumba ikagawanika pa iyo yokha, sikhoza kukhazikika nyumbayo, Ndipo Satana akadziukira mwini yekha, nagawanika, sakhoza kukhazikika, koma atsirizika. Komatu palibe munthu akhoza kulowa m'nyumba ya mwini mphamvu, ndi kufunkha akatundu ake, koma athange wamanga mwini mphamvuyo; ndipo pamenepo adzafunkha za m'nyumba mwake. Indetu, ndinena ndi inu, Adzakhululukidwa machimo onse a ana a anthu, ndi zamwano zilizonse adzachita mwano nazo; koma aliyense adzachitira Mzimu Woyera mwano alibe kukhululukidwa nthawi yonse, koma anapalamuladi tchimo losatha; pakuti adanena, Ali ndi mzimu wonyansa. Ndipo anadza amake ndi abale ake; naima kunja, namtumira uthenga kumuitana. Ndipo anthu ambiri anakhala pansi pomzinga; nanena kwa Iye, Onani, amanu ndi abale anu ali kunja akufunani Inu. Ndipo anawayankha nanena, Amai wanga ndi abale anga ndani? Ndipo anawaunguzaunguza iwo akumzingawo, nanena, Taonani, amai wanga ndi abale anga. Pakuti aliyense achita chifuniro cha Mulungu, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo, ndi amai. Ndipo anayambanso kuphunzitsa pambali pa nyanja. Ndipo anasonkhana kwa Iye khamu lalikulukulu, kotero kuti analowa Iye mungalawa, nakhala m'nyanja; ndipo khamu lonse linakhala pamtunda m'mbali mwa nyanja. Ndipo anawaphunzitsa zinthu zambiri m'mafanizo, nanena nao m'chiphunzitso chake, Mverani: taonani, wofesa anatuluka kukafesa; ndipo kunali, m'kufesa kwake, zina zinagwa m'mbali mwa njira, ndi mbalame zinadza ndi kuzitha kudya. Ndipo zina zinagwa pa nthaka yathanthwe, pamene panalibe nthaka yambiri; ndipo pomwepo zinamera, chifukwa zinalibe nthaka yakuya; ndipo litakwera dzuwa zinapserera; ndipo popeza zinalibe mizu zinakhwinyata. Ndipo zina zinagwa paminga, ndipo minga inakula, nizitsamwitsa, ndipo sizinabala zipatso. Ndipo zina zinagwa m'nthaka yabwino, ndipo zinapatsa zipatso, ndi kukula ndi kuchuluka; ndipo zinabala kupindula makumi atatu, ndi makumi asanu ndi limodzi, ndi makumi khumi. Ndipo ananena, Amene ali nao makutu akumva amve. Ndipo pamene anakhala pa yekha, iwo amene anali pafupi ndi Iye pamodzi ndi khumi ndi awiriwo anamfunsa za mafanizo. Ndipo Iye ananena nao, Kwa inu kwapatsidwa chinsinsi cha Ufumu wa Mulungu; koma kwa iwo ali kunja zonse zichitidwa m'mafanizo; kuti kupenya apenye, koma asazindikire; ndipo kumva amve, koma asadziwitse; kuti pena angatembenuke, ndi kukhululukidwa. Ndipo ananena nao, Simudziwa kodi fanizo ili? Mukazindikira bwanji mafanizo onse? Wofesa afesa mau. Ndipo iwo ndiwo a m'mbali mwa njira mofesedwamo mau; ndipo pamene anamva, pomwepo akudza Satana nachotsa mau ofesedwa mwa iwo. Ndipo momwemonso iwo ndiwo amene afesedwa pathanthwe, atamva mau, awalandira pomwepo ndi kusekera; ndipo alibe mizu mwa iwo okha, koma akhala kanthawi; pamenepo pakudza masautso kapena mazunzo chifukwa cha mau, pomwepo akhumudwa. Ndipo ena ndiwo akufesedwa kuminga; iwo ndiwo amene adamva mau, ndipo malabadiro a dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma, ndi kulakalaka kwa zinthu zina, zilowamo, zitsamwitsa mau, ndipo akhala opanda chipatso. Ndipo iwo ofesedwa pa nthaka yabwino ndiwo oterewa akumva mau, nawalandira, nabala zipatso zakupindula makumi atatu, ndi makumi asanu ndi limodzi, ndi makumi khumi. Ndipo ananena ndi iwo, Kodi atenga nyali kuti akaivundikire mbiya, kapena akaiike pansi pa kama, osati kuti akaiike pa choikapo chake? Pakuti kulibe kanthu kobisika, koma kuti kaonetsedwe; kapena kulibe kanthu kanakhala kam'tseri, koma kuti kakaululidwe. Ngati munthu ali nao makutu akumva, amve. Ndipo ananena nao, Yang'anirani chimene mukumva; ndi muyeso umene muyesera nao udzayesedwa kwa inu; ndipo kudzaonjezedwa kwa inu. Pakuti kwa iye amene ali nako kanthu, kadzapatsidwa; ndipo kwa iye amene alibe kanthu, kadzachotsedwa ngakhale kanthu kalikonse ali nako. Ndipo ananena, Ufumu wa Mulungu uli wotero, monga ngati munthu akataya mbeu panthaka; nakagona ndi kuuka, usiku ndi usana, ndipo mbeu zikamera, ndi kukula, iye sadziwa umo zichitira. Nthaka ibala zipatso zake yokha; uyamba mmera, zitsata ngala, pamenepo maso okhwima m'ngalamo. Pakutcha zipatso, pamenepo atenga chisenga, pakuti nthawi yakumweta yafika. Ndipo ananena, Tidzafaniziranji Ufumu wa Mulungu? Kapena tidzaulinganiza ndi fanizo lotani? Ngati mbeu yampiru, imene ikafesedwa panthaka, ingakhale ichepa ndi mbeu zonse za padziko, koma pamene ifesedwa, imera nikula koposa zitsamba zonse, nichita nthambi zazikulu; kotero kuti mbalame za m'mlengalenga zikhoza kubindikira mumthunzi mwake. Ndipo ndi mafanizo otere ambiri analankhula nao mau, monga anakhoza kumva; ndipo sanalankhule nao wopanda fanizo: koma m'tseri anatanthauzira zonse kwa ophunzira ake. Ndipo dzuwa lomwelo, pofika madzulo, ananena kwa iwo, Tiolokere tsidya lina. Ndipo posiya khamulo anamtenga apite nao, monga momwe anali, mungalawa. Ndipo panali ngalawa zina pamodzi ndi Iye. Ndipo panauka namondwe wamkulu wa mphepo, ndi mafunde anagavira mungalawa, motero kuti ngalawa inayamba kudzala. Ndipo Iye mwini anali kutsigiro, nagona tulo pamtsamiro; ndipo anamuutsa Iye nanena kwa Iye, Mphunzitsi, kodi simusamala kuti titayika ife? Ndipo anauka, nadzudzula mphepo, nati kwa nyanja, kuti, Tonthola, khala bata. Ndipo mphepo inaleka, ndipo kunagwa bata lalikulu. Ndipo ananena nao, Muchitiranji mantha? Kufikira tsopano mulibe chikhulupiriro kodi? Ndipo iwo anachita mantha akulu, nanenana wina ndi mnzake, Uyu ndani nanga, kuti ingakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye? Ndipo anafika tsidya lina la nyanja, kudziko la Agerasa. Ndipo pamene adatuluka mungalawa, pomwepo anakomana naye munthu wotuluka kumanda wa mzimu wonyansa, amene anayesa nyumba yake kumanda; ndipo palibe munthu anakhoza kummanganso, inde ngakhale ndi unyolo; pakuti ankamangidwa kawirikawiri ndi matangadza ndi maunyolo, ndipo anamwetula maunyolo, naduladula matangadza; ndipo palibe munthu anali ndi mphamvu yakumfuya. Ndipo masiku onse, usiku ndi usana, anakhala m'manda ndi m'mapiri, nafuula, nadzitematema ndi miyala. Ndipo pakuona Yesu kutali, anathamanga, namgwadira Iye; ndipo anafuula ndi mau olimba, nanena, Ndili ndi chiyani ine ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkulukulu? Ndikulumbirirani pa Mulungu, msandizunze. Pakuti ananena kwa iye, Tuluka iwe, mzimu wonyansa, kwa munthuyu. Ndipo anamfunsa, Dzina lako ndani? Ndipo ananena kwa Iye, Dzina langa ndine Legio; chifukwa tili ambiri. Ndipo anampempha Iye kwambiri kuti asaitulutsire kunja kwake kwa dziko. Ndipo panali pamenepo gulu lalikulu la nkhumba zilinkudya kuphiri. Ndipo inampempha Iye, kuti, Titumizeni ife mu nkhumbazo, kuti tilowe mu izo. Ndipo anailola. Ndipo mizimu yonyansa inatuluka, nilowa mu nkhumba; ndipo gulu linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m'nyanja, ndizo ngati zikwi ziwiri; ndipo zinatsamwa m'nyanja. Ndipo akuziweta anathawa, nauza m'mudzi, ndi kuminda. Ndipo anadza kudzaona chochitikacho. Ndipo anadza kwa Yesu, napenya wogwidwa ziwandayo alikukhala pansi, wovala ndi wa nzeru zake zabwino, ndiye amene anali ndi legio; ndipo anaopa iwo. Ndipo adapenyawo adawafotokozera umo anachitira ndi wogwidwa ziwandayo, ndi za nkhumbazo. Ndipo anayamba kumpempha Iye kuti achoke m'malire ao. Ndipo m'mene Iye analikulowa mungalawa, anampempha waziwanda uja kuti akhale ndi Iye. Ndipo sanamlole, koma ananena naye, Muka kwanu kwa abale ako, nuwauze zinthu zazikulu anakuchitira Ambuye, ndi kuti anakuchitira chifundo. Ndipo anamuka nayamba kulalikira ku Dekapoli zinthu zazikulu Yesu adamchitira iye; ndipo anthu onse anazizwa. Ndipo pamene Yesu anaolokanso mungalawa tsidya lina, khamu lalikulu linasonkhana kwa Iye; ndipo Iye anali pambali pa nyanja. Ndipo anadzako mmodzi wa akulu a sunagoge, dzina lake Yairo; ndipo pakuona Iye, anagwada pa mapazi ake, nampempha kwambiri, nanena, kuti, Kamwana kanga kabuthu kalinkutsirizika; ndikupemphani Inu mufikeko, muike manja anu pa iko, kuti kapulumuke, ndi kukhala ndi moyo. Ndipo ananka naye pamodzi; ndipo khamu lalikulu linamtsata Iye, ndi kumkanikiza Iye. Ndipo munthu wamkazi amene anali ndi nthenda yachidwalire zaka khumi ndi ziwiri, ndipo anamva zowawa zambiri ndi asing'anga ambiri, nalipira zonse anali nazo osachira pang'ono ponse, koma makamaka nthenda yake idakula, m'mene iye anamva mbiri yake ya Yesu, anadza m'khamu kumbuyo kwake, nakhudza chovala chake. Pakuti ananena iye, Ngati ndikakhudza ngakhale zovala zake ndidzapulumutsidwa. Ndipo pomwepo kasupe wa nthenda yake adaphwa; ndipo anazindikira m'thupi kuti anachiritsidwa chivutiko chake. Ndipo pomwepo Yesu, pamene anazindikira mwa Iye yekha kuti mphamvu idatuluka mwa Iye, anapotoloka m'khamu, nanena, Ndani anakhudza zovala zanga? Ndipo ophunzira ake ananena kwa Iye, Muona kuti khamu lilikukanikiza Inu, ndipo munena kodi, Wandikhudza ndani? Ndipo Iye anaunguzaunguza kumuona iye amene adachita ichi. Koma mkaziyo anachita mantha, ndi kunthunthumira, podziwa chimene anamchitira iye, nadza, namgwadira, namuuza choona chonse. Ndipo anati kwa iye, Mwana wamkaziwe, chikhulupiriro chako chakupulumutsa; muka mumtendere, nukhale wochira chivutiko chako. M'mene iye ali chilankhulire, anafika a kunyumba ya mkulu wa sunagoge, nanena, kuti, Mwana wako wafa; uvutiranjinso Mphunzitsi? Koma Yesu wosasamala mau olankhulidwawo, ananena kwa mkulu wa sunagoge, Usaope, khulupirira kokha. Ndipo sanalole munthu yense kutsagana naye, koma Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane mbale wake wa Yakobo. Ndipo anafika kunyumba kwake kwa mkulu wa sunagoge; ndipo anaona chipiringu, ndi ochita maliro, ndi akukuwa ambiri. Ndipo m'mene atalowa, ananena nao, Mubuma ndi kulira bwanji? Mwana sanafe, koma ali m'tulo. Ndipo anamseka Iye pwepwete. Koma Iye anawatulutsa onse, natenga atate wa mwana, ndi amake, ndi ajawo anali naye, nalowa m'mene munali mwanayo. Ndipo anagwira dzanja lake la mwana, nanena kwa iye, Talita koumi, ndiko kunena posandulika, Buthu, ndinena ndi iwe, Uka. Ndipo pomwepo buthulo linauka, niliyenda; pakuti linali la zaka khumi ndi ziwiri. Ndipo anadabwa pomwepo ndi kudabwa kwakukulu. Ndipo anawalamulira kwambiri kuti asadziwe ichi munthu mmodzi, nawauza kuti ampatse iye kudya. Ndipo Iye anatuluka kumeneko; nafika kudziko la kwao; ndipo ophunzira ake anamtsata. Ndipo pofika tsiku la Sabata, anayamba kuphunzitsa m'sunagoge; ndipo ambiri anamva Iye, nazizwa, nanena, Uyu adazitenga kuti izi? Nzeru yopatsidwa kwa munthuyu njotani, ndi zamphamvu zotere zochitidwa ndi manja ake? Si mmisiri wa mitengo uyu, mwana wa Maria, mbale wao wa Yakobo, ndi Yose, ndi Yudasi, ndi Simoni? Ndipo alongo ake sali nafe pano kodi? Ndipo anakhumudwa ndi Iye. Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Mneneri sakhala wopanda ulemu, koma m'dziko la kwao ndimo, ndi pakati pa abale ake, ndi m'nyumba yake. Ndipo kumeneko sanakhoze Iye kuchita zamphamvu konse, koma kuti anaika manja ake pa anthu odwala owerengeka, nawachiritsa. Ndipo anazizwa chifukwa cha kusakhulupirira kwao. Ndipo anayendayenda m'midzi yozungulirapo, naphunzitsa. Ndipo anadziitanira khumi ndi awiriwo, nayamba kuwatumiza iwo awiriawiri; nawapatsa mphamvu pa mizimu yonyansa; ndipo anawauza kuti asatenge kanthu ka paulendo, koma ndodo yokha; asatenge mkate, kapena thumba, kapena ndalama m'lamba lao; koma avale nsapato; ndipo anati, Musavale malaya awiri. Ndipo ananena nao, Kumene kulikonse mukalowa m'nyumba, khalani komweko kufikira mukachokako. Ndipo pamalo ponse sakulandirani, kapena kumvera inu, pakuchoka kumeneko, sansani fumbi lili kumapazi anu, likhale mboni ya kwa iwo. Ndipo anatuluka nalalikira kuti anthu atembenuke mitima. Ndipo anatulutsa ziwanda zambiri, nadzoza mafuta anthu ambiri akudwala, nawachiritsa. Ndipo mfumu Herode anamva izi; pakuti dzina lake lidamveka; ndipo ananena, kuti, Yohane Mbatizi wauka kwa akufa, ndipo chifukwa chake mphamvu izi zichitachita mwa Iye. Koma ena ananena, kuti, Ndiye Eliya. Anati enanso, Ndiye mneneri, monga ngati mmodzi wa aneneriwo. Koma Herode pamene anamva, ananena, Yohane amene ndamdula mutu, wauka iyeyo. Pakuti Herode, mwini yekha, adatuma anthu namgwira Yohane, nammanga m'nyumba yandende, chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa Filipo mbale wake; chifukwa adamkwatira iye. Pakuti Yohane adanena kwa Herode, Si kuloledwa kwa inu kukhala naye mkazi wa mbale wanu. Ndipo Herodiasi anamuda, nafuna kumupha; koma sanakhoze; pakuti Herode anaopa Yohane, podziwa kuti ali munthu wolungama ndi woyera mtima, ndipo anamsunga iye. Ndipo pamene anamva iye anathedwa nzeru, nakondwa kumva iye. Ndipo pamene panafika tsiku loyenera, tsiku la kubadwa kwake kwa Herode, iye anawakonzera phwando akulu ake ndi akazembe ake ndi anthu omveka a ku Galileya; ndipo pamene mwana wamkazi wa Herodiasi analowa yekha navina, anakondwetsa Herode ndi iwo akukhala naye pachakudya; ndipo mfumuyo inati kwa buthulo, Tapempha kwa ine chilichonse uchifuna, ndidzakupatsa iwe. Ndipo anamlumbirira iye, kuti, Chilichonse ukandipempha ndidzakupatsa, kungakhale kukugawira ufumu wanga. Ndipo anatuluka, nati kwa amake, Ndidzapempha chiyani? Ndipo iye anati, Mutu wake wa Yohane Mbatizi. Ndipo pomwepo analowa m'mangum'mangu kwa mfumu, napempha kuti, Ndifuna kuti mundipatse tsopano apa, mutu wake wa Yohane Mbatizi mumbale. Ndipo mfumu inamva chisoni chachikulu; koma chifukwa cha malumbiro ake, ndi cha iwo akukhala pachakudya, sanafune kumkaniza. Ndipo pomwepo mfumu inatuma mnyamata, namlamulira akatenge mutu wake; ndipo iye anamuka namdula mutu m'nyumba yandende; natengera mutu wake mumbale, naupereka kwa buthulo; ndipo buthu linaupereka kwa amake. Ndipo m'mene ophunzira ake anamva, anadza nanyamula mtembo wake nauika m'manda. Ndipo atumwi anasonkhana kwa Yesu; namuuza zilizonse adazichita, ndi zonse adaziphunzitsa. Ndipo Iye ananena nao, idzani inu nokha padera ku malo achipululu, mupumule kamphindi. Pakuti akudza ndi akuchoka anali piringupiringu, ndipo analibe nthawi yokwanira kudya. Ndipo anachokera m'ngalawa kunka kumalo achipululu padera. Ndipo anthu anawaona alikumuka, ndipo ambiri anawazindikira, nathamangira limodzi kumeneko pamtunda, ochokera m'midzi monse, nawapitirira. Ndipo anatuluka Iye, naona khamu lalikulu la anthu, nagwidwa chifundo ndi iwo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri. Ndipo pamene dzuwa lidapendeka ndithu, anadza kwa Iye ophunzira ake, nanena, Malo ano nga chipululu, ndi dzuwa lapendeka ndithu; muwauze kuti amuke, alowe kumilaga ndi kumidzi yozungulira, akadzigulire okha kanthu kakudya. Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Apatseni kudya ndinu. Ndipo iwo ananena naye, Kodi tikapita ife ndi kugula mikate ya pa marupiya atheka mazana awiri, ndi kuwapatsa kudya? Ndipo Iye ananena nao, kuti, Muli nayo mikate ingati? Pitani, mukaone. Ndipo m'mene anadziwa ananena, Isanu, ndi nsomba ziwiri. Ndipo anawalamulira kuti akhalitse pansi onse magulumagulu pamsipu. Ndipo anakhala pansi mabungwemabungwe a makumi khumi, ndi a makumi asanu. Ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo nayang'ana kumwamba, nadalitsa, nagawa mikate; napatsa kwa ophunzira kuti apereke kwa iwo; ndi nsomba ziwiri anagawira onsewo. Ndipo anadya iwo onse, nakhuta. Ndipo anatola makombo, madengu khumi ndi iwiri, ndiponso za nsomba. Ndipo amene anadya mikate iyo anali amuna zikwi zisanu. Ndipo pomwepo Iye anakakamiza ophunzira ake alowe m'ngalawa, ndi kumtsogolera kutsidya lija ku Betsaida, m'mene Iye yekha alimkuuza khamulo kuti amuke. Ndipo atalawirana nao, anachoka Iye, nalowa m'phiri kukapemphera. Ndipo pofika madzulo ngalawa inali pakati pa nyanja, ndi Iye yekha pamtunda. Ndipo pakuwaona ali kuvutidwa ndi kupalasa, pakuti mphepo inadza nikomana nao, pa ulonda wachinai wa usiku Iye anadza kwa iwo, alikuyenda pamwamba pa nyanja; nati awapitirire; koma iwo, pamene anamuona alikuyenda panyanja, anayesa kuti ndi mzukwa, nafuula: pakuti iwo onse anamuona Iye, nanthunthumira. Koma pomwepo anawalankhula nanena nao, Limbani mtima; ndinetu, musaope. Ndipo Iye anakwera, nalowa kwa iwo m'ngalawa, ndipo mphepo inaleka; ndipo anadabwa kwakukulu mwa iwo okha; pakuti sanazindikire za mikateyo, koma mitima yao inauma. Ndipo ataoloka iwo, anafika pamtunda ku Genesarete, nakocheza padooko. Ndipo pamene anatuluka m'ngalawa anamzindikira pomwepo, nathamangira dziko lonselo nayamba kunyamula anthu odwala pa mphasa zao, kufika nao kumene anamva kuti analiko Iye. Ndipo kumene konse adalowa Iye m'midzi, kapena m'mizinda, kapena m'milaga, anthu anagoneka odwala pamisika, nampempha Iye kuti akakhudze ngakhale mphonje yokha ya chovala chake; ndipo onse amene anamkhudza anachiritsidwa. Ndipo anasonkhana kwa Iye Afarisi, ndi alembi ena, akuchokera ku Yerusalemu, ndipo anaona kuti ophunzira ake ena anadya mkate ndi m'manja mwakuda, ndiwo osasamba. Pakuti Afarisi, ndi Ayuda onse sakudya osasamba m'manja ao, kuti asungire mwambo wa akulu; ndipo pakuchoka kumsika, sakudya osasamba m'thupi; ndipo zilipo zinthu zina zambiri anazilandira kuzisunga, ndizo matsukidwe a zikho, ndi miphika, ndi zotengera zamkuwa. Ndipo Afarisi ndi alembi anamfunsa Iye, kuti, Bwanji ophunzira anu satsata mwambo wa akulu, koma akudya mkate wao ndi m'manja mwakuda? Ndipo Iye ananena nao, Yesaya ananenera bwino za inu onyenga, monga mwalembedwa, Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao, koma mtima wao ukhala kutali ndi Ine. Koma andilambira Iye kwachabe, ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu. Musiya lamulo la Mulungu, nimusunga mwambo wa anthu. Ndipo ananena nao, Bwino mukaniza lamulo la Mulungu, kuti musunge mwambo wanu. Pakuti Mose anati, Lemekeza atate wako ndi amai ako; ndipo iye wakunenera zoipa atate wake kapena amai wake, afe ndithu; koma inu munena, Munthu akati kwa atate wake, kapena amai wake, Korban, ndiko kuti Mtulo, chimene ukadathandizidwa nacho ndi ine, simulolanso kumchitira kanthu atate wake kapena amai wake; muyesa achabe mau a Mulungu mwa mwambo wanu, umene munaupereka: ndi zinthu zotere zambiri muzichita. Ndipo anadziitaniranso khamu la anthu, nanena nao, Mverani Ine nonsenu, ndipo dziwitsani: kulibe kanthu kunja kwa munthu kukalowa mwa iye, kangathe kumdetsa: koma zinthu zakutuluka mwa munthu, ndizo zakumdetsa munthu. *** Ndipo m'mene Iye adalowa m'nyumba kusiyana ndi khamulo, ophunzira ake anamfunsa Iye fanizolo. Ndipo ananena nao, Mutero inunso opanda nzeru kodi? Kodi simuzindikira kuti kanthu kalikonse kochokera kunja kukalowa mwa munthu, sikangathe kumdetsa iye; chifukwa sikalowa mumtima mwake, koma m'mimba mwake, ndipo katulukira kuthengo? Ndipo potero anayeretsa zakudya zonse. Ndipo anati, Chotuluka mwa munthu ndicho chidetsa munthu. Pakuti m'kati mwake mwa mitima ya anthu, mutuluka maganizo oipa, zachiwerewere, zakuba, zakupha, zachigololo, masiriro, zoipa, chinyengo, chinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa: zoipa izi zonse zituluka m'kati, nizidetsa munthu. Ndipo Iye anauka nachoka kumeneko, nanka ku maiko a ku Tiro ndi Sidoni. Ndipo analowa m'nyumba, nafuna kuti asadziwe anthu; ndipo sanakhoze kubisika. Koma pomwepo mkazi, kabuthu kake kanali ndi mzimu wonyansa, pamene anamva za Iye, anadza, nagwa pa mapazi ake. Koma mkaziyo anali Mgriki, mtundu wake Msiro-Fenisiya. Ndipo anampempha Iye kuti atulutse chiwanda m'mwana wake. Ndipo ananena naye, Baleka, athange akhuta ana; pakuti si kwabwino kuti titenge mkate wa ana, ndi kuutayira tiagalu. Koma iye anavomera nanena ndi Iye, Ine Ambuye; tingakhale tiagalu ta pansi pa gome tikudyako nyenyeswa za ana. Ndipo anati kwa iye, Chifukwa cha mau amene, muka; chiwanda chatuluka m'mwana wako wamkazi. Ndipo anachoka kunka kunyumba kwake, napeza mwana atamgoneka pakama, ndi chiwanda chitatuluka. Ndipo anatulukanso m'maiko a ku Tiro, nadzera pakati pa Sidoni, kufikira ku nyanja ya Galileya, ndi kupyola pakati pa maiko a ku Dekapoli. Ndipo anadza naye kwa Iye munthu wogontha, ndi wachibwibwi; ndipo anampempha Iye kuti aike dzanja pa iye. Ndipo anampatula pa khamu la anthu pa yekha, nalonga zala zake m'makutu mwake, nalavula malovu, nakhudza lilime lake: nagadamira kumwamba, nausa moyo, nanena naye, Efata, ndiko, Tatseguka. Ndipo makutu ake anatsegula, ndi chomangira lilime lake chinamasulidwa, ndipo analankhula chilunjikire. Ndipo anawalamulira kuti asauze munthu aliyense; koma monga momwe Iye anawalamulitsa momwenso makamaka analalikira kopambana. Ndipo anadabwa kwakukulukulu, nanena, Wachita Iye zonse bwino; angakhale ogontha awamvetsa, ndi osalankhula awalankhulitsa. Masiku ajawo pakukhalanso khamu lalikulu la anthu, ndipo analibe kanthu kakudya, Iye anadziitanira ophunzira ake, nanena nao, Ndimva nalo chifundo khamulo, chifukwa ali ndi Ine chikhalire masiku atatu, ndipo alibe kanthu kakudya: ndipo ngati ndiwauza iwo amuke kwao osadya kanthu, adzakomoka panjira; ndipo ena a iwo achokera kutali. Ndipo ophunzira ake anamyankha Iye, kuti, Munthu adzatha kutenga kuti mikate yakukhutitsa anthu awa m'chipululu muno? Ndipo anawafunsa, Muli nayo mikate ingati? Ndipo anati, Isanu ndi iwiri. Ndipo analamulira anthu a khamulo akhale pansi; natenga mikate isanu ndi iwiriyo, nayamika, nanyema, napatsa ophunzira ake, kuti apereke kwa iwo; ndipo anapereka kwa khamulo. Ndipo anali nato tinsomba towerengeka; ndipo Iye anatidalitsa, nati atipereke itonso. Ndipo anadya nakhuta; ndipo anatola makombo madengu asanu ndi awiri. Ndipo iwo anali ngati zikwi zinai; ndipo Iye analawirana nao. Ndipo pomwepo analowa m'ngalawa ndi ophunzira ake, nafika ku mbali ya ku Dalamanuta. Ndipo Afarisi anatuluka, nayamba kufunsana naye, ndi kufuna kwa Iye chizindikiro chochokera Kumwamba, namuyesa Iye. Ndipo anausitsa moyo m'mzimu wake, nanena, Anthu a mbadwo uno afunafuna chizindikiro bwanji? Indetu ndinena kwa inu, ngati chizindikiro chidzapatsidwa kwa mbadwo uno! Ndipo anawasiya iwo, nalowanso m'ngalawa, nachoka kunka ku tsidya lija. Ndipo ophunzira adaiwala kutenga mikate, ndipo analibe mkate m'ngalawa koma umodzi wokha. Ndipo Iye anawalamula, nanena, Yang'anirani, penyani kuti mupewe chotupitsa mkate cha Afarisi, ndi chotupitsa mkate cha Herode. Ndipo anatsutsana wina ndi mnzake, nanena kuti, Tilibe mikate. Ndipo Yesu pamene anazindikira, ananena nao, Bwanji mutsutsana chifukwa mulibe mkate? Kodi kufikira tsopano simuzindikira, nisimudziwitsa? Kodi muli nayo mitima yanu youma? Pokhala nao maso simupenya kodi? Ndi pokhala nao makutu simukumva kodi? Ndipo simukumbukira kodi? Pamene ndinawagawira anthu zikwi zisanu mikate isanu ija, munatola madengu angati odzala ndi makombo? Ananena naye, Khumi ndi iwiri. Ndipo mikate isanu ndi iwiri kwa anthu zikwi zinai, munatola madengu angati odzala ndi makombo? Ndipo ananena naye, Asanu ndi awiri. Ndipo Iye ananena nao, Simudziwitsa ngakhale tsopano kodi? Ndipo anadza ku Betsaida. Ndipo anadza naye kwa Iye munthu wakhungu, nampempha Iye kuti amkhudze. Ndipo anamgwira dzanja munthu wakhunguyo, natulukira naye kunja kwa mudzi; ndipo atamthira malovu m'maso mwake, naika manja pa iye, anamfunsa, Uona kanthu kodi? Ndipo anakweza maso, nanena, Ndiona anthu; pakuti ndiwapenya ayendayenda ngati mitengo. Pamenepo anaikanso manja m'maso mwake; ndipo anapenyetsa, nachiritsidwa, naona zonse mbee. Ndipo anamtumiza amuke kwao, nanena, Usalowe konse m'mudzi. Ndipo anatuluka Yesu, ndi ophunzira ake, nalowa kumidzi ya ku Kesareya-Filipi; ndipo panjira anafunsa ophunzira ake, nanena nao, Kodi anthu ananena kuti Ine ndine yani? Ndipo ananena, nati, Yohane Mbatizi; ndi ena, Eliya; koma ena, Mmodzi wa aneneri. Ndipo Iye anawafunsa, Koma inu munena kuti ndine yani? Petro anayankha nanena naye, Ndinu Khristu. Ndipo anawauzitsa iwo kuti asanene kwa munthu mmodzi za Iye. Ndipo anayamba kuwaphunzitsa, kuti kuyenera kuti Mwana wa Munthu akamve zowawa zambiri, nakakanidwe ndi akulu ndi ansembe aakulu, ndi alembi, nakaphedwe, ndipo mkucha wake akauke. Ndipo mauwo ananena poyera. Ndipo Petro anamtenga Iye, nayamba kumdzudzula. Koma Iye anapotoloka, napenya ophunzira ake, namdzudzula Petro, nanena, Choka, pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; popeza susamalira zinthu za Mulungu, koma za anthu. Ndipo anadziitanira khamulo la anthu pamodzi ndi ophunzira ake, nati kwa iwo, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule mtanda wake, nanditsate Ine. Pakuti yense wakufuna kupulumutsa moyo wake adzautaya; ndipo yense wakutaya moyo wake chifukwa cha Ine, ndi chifukwa cha Uthenga Wabwino, adzaupulumutsa. Pakuti munthu apindulanji akadzilemezera dziko lonse, natayapo moyo wake? Pakuti munthu akapereka chiyani chosintha nacho moyo wake? Pakuti yense wakuchita manyazi chifukwa cha Ine, ndi cha mau anga mu mbadwo uno wachigololo ndi wochimwa, Mwana wa Munthu adzachitanso manyazi chifukwa cha iyeyu, pamene Iye adzafika nao angelo ake oyera, mu ulemerero wa Atate wake. Ndipo ananena nao, Ndithu ndinena ndi inu kuti, Alipo ena akuimirira pano, amene sadzalawa imfa konse, kufikira akaona Ufumu wa Mulungu utadza ndi mphamvu. Ndipo atapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu anatenga Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, nakwera nao pa phiri lalitali padera pa okha; ndipo anasandulika pamaso pao: ndipo zovala zake zinakhala zonyezimira, zoyera mbu; monga ngati muomba wotsuka nsalu pa dziko lapansi sangathe kuziyeretsai. Ndipo anaonekera kwa iwo Eliya ndi Mose, alikulankhulana ndi Yesu. Ndipo Petro anayankha, nanena ndi Yesu, Rabi, kutikomera ife kukhala pano; ndipo timange misasa itatu; umodzi wa inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya. Pakuti sanadziwe chimene adzayankha; chifukwa anachita mantha ndithu. Ndipo panadza mtambo wakuwaphimba iwo; ndipo mau munatuluka m'mtambomo, kuti, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa; mverani Iye. Ndipo dzidzidzi pounguzaunguza, sanapenye munthu wina yense, koma Yesu yekha, ndi iwo eni. Ndipo pakutsika iwo paphiri, Iye anawalamula kuti asauze munthu zinthu zimene adaziona, koma pamene Mwana wa Munthu akadzauka kwa akufa. Ndipo anasunga mauwo, nafunsana mwa iwo okha, kuti, Kuuka kwa akufa nchiyani? Ndipo anamfunsa Iye, nanena, Nanga alembi anena kuti adzayamba kufika Eliya? Ndipo Iye ananena nao, Eliya ayamba kudza ndithu, nadzakonza zinthu zonse; ndipo kwalembedwa bwanji za Mwana wa Munthu, kuti ayenera kumva zowawa zambiri ndi kuyesedwa chabe? Koma ndinena ndi inu kuti anafikadi Eliya, ndipo anamchitiranso zilizonse iwo anazifuna, monga kwalembedwa za iye. Ndipo pamene anadza kwa ophunzira, anaona khamu lalikulu la anthu ozungulira iwo, ndi alembi alikufunsana nao. Ndipo pomwepo anthu onse a khamulo, pakumuona Iye, anazizwa kwambiri, namthamangira Iye, namlonjera. Ndipo anawafunsa iwo, Mufunsana nao chiyani? Ndipo wina wa m'khamulo anamyankha Iye, kuti, Mphunzitsi, ndadza naye kwa Inu mwana wanga, ali nao mzimu wosalankhula; ndipo ponse pamene umgwira, umgwetsa; ndipo achita thovu, nakukuta mano, nanyololoka; ndipo ndinalankhula nao ophunzira anu kuti autulutse; koma sanakhoze. Ndipo Iye anawayankha nanena, Mbadwo wosakhulupirira inu, ndidzakhala ndi inu kufikira liti? Ndidzakulekererani nthawi yanji? Mudze naye kwa Ine. Ndipo anadza naye kwa Iye; ndipo pakumuona, pomwepo mzimuwo unamng'amba koopsa; ndipo anagwa pansi navimvinika ndi kuchita thovu. Ndipo Iye anafunsa atate wake, kuti, Chimenechi chinayamba kumgwira liti? Ndipo anati, Chidamyamba akali mwana. Ndipo kawirikawiri ukamtaya kumoto ndi kumadzi, kumuononga; koma ngati mukhoza kuchita kanthu mtithandize, ndi kutichitira chifundo. Ndipo Yesu ananena naye, Ngati mukhoza! Zinthu zonse zitheka ndi iye wakukhulupirira. Pomwepo atate wa mwana anafuula, nanena, Ndikhulupirira; thandizani kusakhulupirira kwanga. Ndipo pamene Yesu anaona kuti khamu la anthu lilikuthamangira pamodzi, anadzudzula mzimu woipawo, nanena ndi uwo, Mzimu wosalankhula ndi wogontha iwe, Ine ndikulamula iwe, tuluka mwa iye, ndipo usalowenso mwa iye. Ndipo pamene unafuula, numng'ambitsa, unatuluka; ndipo mwana anakhala ngati wakufa; kotero kuti ambiri ananena, Wamwalira. Koma Yesu anamgwira dzanja lake, namnyamutsa; ndipo anaimirira. Ndipo pamene Iye adalowa m'nyumba, ophunzira ake anamfunsa m'tseri, kuti, Nanga bwanji sitinakhoza ife kuutulutsa? Ndipo Iye anati kwa iwo, Mtundu uwu sukhoza kutuluka ndi kanthu kena konse, koma ndi kupemphera. Ndipo anachoka iwo kumeneko, napyola pakati pa Galileya; ndipo Iye sanafune kuti munthu adziwe. Pakuti anaphunzitsa ophunzira ake, nanena nao, kuti, Mwana wa Munthu aperekedwa m'manja anthu, ndipo adzamupha Iye; ndipo ataphedwa, adzauka pofika masiku atatu. Koma iwo sanazindikire mauwo, naopa kumfunsa. Ndipo iwo anadza ku Kapernao; ndipo pamene anakhala m'nyumba, Iye anawafunsa, Munalikutsutsana ninji panjira? Koma iwo anakhala chete; pakuti anatsutsana wina ndi mnzake panjira, kuti, wamkulu ndani? Ndipo m'mene anakhala pansi anaitana khumi ndi awiriwo; nanena nao, Ngati munthu afuna kukhala woyamba, akhale wakuthungo wa onse, ndi mtumiki wa onse. Ndipo anatenga kamwana, nakaika pakati pao, nakayangata, nanena nao, Munthu aliyense adzalandira kamodzi ka tiana totere chifukwa cha dzina langa, alandira Ine; ndipo yense amene akalandira Ine, salandira Ine, koma Iye amene anandituma Ine. Yohane anati kwa Iye, Mphunzitsi, tinaona munthu alikutulutsa ziwanda m'dzina lanu; ndipo tinamletsa, chifukwa sanalikutsata ife. Koma Yesu anati, Musamamletsa iye; pakuti palibe munthu adzachita champhamvu m'dzina langa, nadzakhoza msanga kundinenera Ine zoipa. Pakuti iye wosatsutsana ndi ife athandizana nafe. Pakuti munthu aliyense adzakumwetsani inu chikho cha madzi m'dzina langa chifukwa muli ake a Khristu, indetu ndinena ndi inu, kuti iye sadzataya konse mphotho yake. Ndipo yense amene adzalakwitsa kamodzi ka tiana timeneto takukhulupirira Ine, kuli kwabwino kwa iye makamaka kuti mwala waukulu wamphero ukolowekedwe m'khosi mwake, naponyedwe iye m'nyanja. Ndipo ngati dzanja lako likulakwitsa iwe, ulidule: nkwabwino kwa iwe kulowa m'moyo wopunduka dzanja, koposa kukhala ndi manja ako awiri ndi kulowa m'Gehena, m'moto wosazima. *** Ndipo ngati phazi lako likulakwitsa, ulidule; kulowa iwe m'moyo wopunduka mwendo, kuli kwabwino koposa ndi kukhala ndi mapazi ako awiri ndi kuponyedwa m'Gehena. *** Ndipo ngati diso lako likulakwitsa ulikolowole; kulowa iwe m'Ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi kuli kwabwino koposa ndi kukhala ndi maso awiri ndi kuponyedwa m'Gehena; kumeneko mphutsi yao siikufa, ndi moto suzimidwa. Pakuti onse adzathiridwa mchere wamoto. Mchere uli wabwino; koma ngati mchere unasukuluka, mudzaukoleretsa ndi chiyani? Khalani nao mchere mwa inu nokha, ndipo khalani ndi mtendere wina ndi mnzake. Ndipo ananyamuka Iye kumeneko, nadza ku maiko a ku Yudeya ndi ku tsidya lija la Yordani; ndipo anasonkhananso kwa Iye makamu a anthu; ndipo monga anazolowera, anawaphunzitsanso. Ndipo anadza kwa Iye Afarisi, namfunsa Iye ngati kuloledwa kuti munthu achotse mkazi wake, namuyesa Iye. Ndipo Iye anayankha nati kwa iwo, Kodi Mose anakulamulani chiyani? Ndipo anati, Mose analola kulembera kalata wakulekanira, ndi kumchotsa. Koma Yesu anati kwa iwo, Chifukwa cha kuuma kwa mitima yanu anakulemberani lamulo ili. Koma kuyambira pa chiyambi cha malengedwe anawapanga mwamuna ndi mkazi. Chifukwa chake mwamuna adzasiya atate wake ndi amai wake, ndipo adzaphatikizana ndi mkazi wake; ndipo awiriwa adzakhala thupi limodzi: kotero kuti salinso awiri, koma thupi limodzi. Chifukwa chake chimene Mulungu anachimanga pamodzi, asachilekanitse munthu. Ndipo m'nyumba ophunzira anamfunsanso za chinthu ichi. Ndipo Iye ananena nao, Munthu aliyense akachotsa mkazi wake, nakakwatira wina, achita chigololo kulakwira mkaziyo; ndipo ngati mkazi akachotsa mwamuna wake, nakwatiwa ndi wina, achita chigololo iyeyu. Ndipo analinkudza nato kwa Iye tiana, kuti akatikhudze; ndipo ophunzirawo anawadzudzula. Koma pamene Yesu anaona anakwiya, ndipo anati kwa iwo, Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse: pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa totere. Ndithu ndinena ndi inu, Munthu aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana, sadzalowamo konse. Ndipo Iye anatiyangata, natidalitsa, ndi kuika manja ake pa ito. Ndipo pamene Iye anatuluka kutsata njira, anamthamangira munthu, namgwadira Iye, namfunsa, Mphunzitsi wabwino, ndidzachita chiyani kuti ndilandire moyo wosatha? Ndipo Yesu anati kwa iye, Unditcha Ine wabwino bwanji? Palibe wabwino koma mmodzi, ndiye Mulungu. Udziwa malamulo: Usaphe, Usachite chigololo, Usabe, Usachite umboni wakunama, Usanyenge, Lemekeza atate wako ndi amai ako. Ndipo iye anati kwa Iye, Mphunzitsi, zonsezi ndinazisunga kuyambira ndili mwana. Ndipo Yesu anamyang'ana, namkonda, nati kwa iye, Chinthu chimodzi chikusowa: pita, gulitsa zonse uli nazo, nuzipereke kwa anthu aumphawi, ndipo chuma udzakhala nacho m'mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine. Koma nkhope yake inagwa pa mau awa, ndipo anachoka iye wachisoni; pakuti anali mwini chuma chambiri. Ndipo Yesu anaunguzaunguza, nanena ndi ophunzira ake, Okhala nacho chuma adzalowa mu Ufumu wa Mulungu ndi kuvuta nanga! Ndipo ophunzirawo anazizwa ndithu ndi mau ake. Koma Yesu anayankhanso nanena nao, Ananu, nkovuta ndithu kwa iwo akutama chuma kulowa mu Ufumu wa Mulungu! Nkwa pafupi kuti ngamira ipyole diso la singano kuposa kuti mwini chuma alowe mu Ufumu wa Mulungu. Ndipo anadabwa, nanena kwa Iye, Ndipo angathe kupulumuka ndani? Yesu anawayang'ana iwo nati, Sikutheka ndi anthu, koma kutheka ndi Mulungu; pakuti zinthu zonse zitheka ndi Mulungu. Petro anayamba kunena naye, Onani, ife tinasiya zonse, ndipo tinakutsatani Inu. Yesu anati, Ndithu ndinena ndi inu, Palibe munthu anasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amai, kapena atate, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha Ine, ndi chifukwa cha Uthenga Wabwinowo, amene sadzalandira makumi khumi tsopano nthawi yino, nyumba, ndi abale, ndi alongo, ndi amai, ndi ana, ndi minda, pamodzi ndi mazunzo; ndipo nthawi ilinkudza, moyo wosatha. Koma ambiri akuyamba adzakhala akuthungo, ndi akuthungo adzakhala oyamba. Ndipo iwo anali m'njira alinkukwera kunka ku Yerusalemu; ndipo Yesu analikuwatsogolera; ndipo iwo anazizwa; ndipo akumtsatawo anachita mantha. Ndipo Iye anatenganso khumi ndi awiriwo, nayamba kuwauza zinthu zimene zidzamfikira Iye, nati, Taonani, tikwera ku Yerusalemu; ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi; ndipo iwo adzamweruza kuti ayenera imfa, nadzampereka Iye kwa anthu a mitundu; ndipo adzamnyoza Iye, nadzamthira malovu, nadzamkwapula Iye, nadzamupha; ndipo pofika masiku atatu adzauka. Ndipo anadza kwa Iye Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedeo, nanena naye, Mphunzitsi, tifuna kuti mudzatichitire chimene chilichonse tidzapempha kwa Inu. Ndipo Iye anati kwa iwo, Mufuna kuti ndidzakuchitireni inu chiyani? Ndipo iwo anati kwa Iye, Mutipatse ife kuti tikhale mmodzi kudzanja lanu lamanja, ndi wina kulamanzere, m'ulemerero wanu. Koma Yesu anati kwa iwo, Simudziwa chimene muchipempha. Mukhoza kodi kumwera chikho chimene ndimwera Ine? Kapena kubatizidwa ndi ubatizo umene ndibatizidwa nao Ine? Ndipo anati kwa Iye, Tikhoza. Ndipo Yesu anati kwa iwo, Chikho chimene ndimwera Ine mudzamwera; ndipo ubatizo umene ndibatizidwa nao Ine, mudzabatizidwa nao; koma kukhala kudzanja langa lamanja, kapena lamanzere sikuli kwanga kupatsa; koma kuli kwa iwo amene adawakonzeratu. Ndipo pamene khumiwo anamva, anayamba kupsa mtima chifukwa cha Yakobo ndi Yohane. Ndipo Yesu anawaitana, nanena nao, Mudziwa kuti iwo amene ayesedwa ambuye a mitundu ya anthu amachita ufumu pa iwo; ndipo akulu ao amachita ulamuliro pa iwo. Koma mwa inu sikutero ai; koma amene aliyense afuna kukhala wamkulu mwa inu adzakhala mtumiki wanu; ndipo amene aliyense afuna kukhala woyamba mwa inu adzakhala kapolo wa onse. Pakuti ndithu, Mwana wa Munthu sanadze kutumikiridwa, koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la kwa anthu ambiri. Ndipo iwo anafika ku Yeriko; ndipo m'mene Iye analikutuluka m'Yeriko, ndi ophunzira ake, ndi khamu lalikulu la anthu, mwana wa Timeo, Baratimeo, wopempha wakhungu, analikukhala pansi m'mbali mwa njira. Ndipo pamene anamva kuti ndi Yesu wa ku Nazarete, anayamba kufuula, ndi kunena, Yesu, Inu Mwana wa Davide, mundichitire ine chifundo. Ndipo ambiri anamulamula kuti atonthole: koma makamaka anafuulitsa kuti, Inu mwana wa Davide, mundichitire chifundo. Ndipo Yesu anaima, nati, Mwitaneni. Ndipo anaitana wakhunguyo, nanena naye, Limba mtima; nyamuka, akuitana. Ndipo iye anataya chofunda chake, nazunzuka, nadza kwa Yesu. Ndipo Yesu anamyankha, nati, Ufuna kuti ndikuchitire chiyani? Ndipo wakhunguyo anati kwa Iye, Raboni, ndilandire kuona kwanga. Ndipo Yesu anati kwa iye, Muka; chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe. Ndipo pomwepo anapenyanso; namtsata Iye panjira. Ndipo pamene iwo anayandikira ku Yerusalemu, ku Betefage ndi Betaniya, pa phiri la Azitona, anatuma awiri a ophunzira ake, nanena nao, Mukani, lowani m'mudzi wapandunji ndi inu; ndipo pomwepo pakulowamo mudzapeza mwana wa bulu womangidwa, amene palibe munthu anakhalapo kale lonse; mmasuleni, ndipo mubwere naye. Ndipo munthu akati kwa inu, Mutero bwanji? Katini, Ambuye amfuna iye; ndipo pomwepo adzamtumiza kuno. Ndipo anachoka, napeza mwana wa bulu womangidwa pakhomo, pabwalo m'khwalala, nammasula iye. Ndipo ena akuima kumeneko ananena nao, Muchita chiyani ndi kumasula mwana wa bulu? Ndipo anati kwa iwo monga momwe ananena Yesu: ndipo anawalola iwo apite naye. Ndipo anabwera naye mwana wa bulu kwa Yesu, naika zovala zao pa iye, ndipo Iye anakhala pamenepo. Ndimo ambiri anayala zovala zao panjira; ndi ena zitsamba, anazidula m'minda. Ndipo akutsogolera, ndi iwo akutsata, anafuula, Hosana; Wolemekezeka Iye wakudza m'dzina la Ambuye: Wolemekezeka Ufumu ulinkudza, wa atate wathu Davide; Hosana m'Kumwambamwamba. Ndipo Iye analowa m'Yerusalemu, m'Kachisi; ndipo m'mene anaunguza zinthu zonse, popeza ndi madzulo, anatuluka kupita ku Betaniya pamodzi ndi khumi ndi awiriwo. Ndipo m'mawa mwake, atatuluka ku Betaniya, Iye anamva njala. Ndipo anaona mkuyu kutali, uli ndi masamba; ndipo anadza Iye, kuti kapena akapezapo kanthu: ndipo m'mene anafikako anapeza palibe kanthu koma masamba okha; pakuti siinali nyengo yake ya nkhuyu. Ndipo anayankha nanena ndi uwo, Munthu sadzadyanso zipatso zako nthawi zonse. Ndipo ophunzira ake anamva. Ndipo anafika iwo ku Yerusalemu; ndipo Iye analowa m'Kachisi, nayamba kutulutsa akugulitsa ndi akugula malonda m'Kachisimo, nagubuduza magome a osinthana ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda; ndipo sanalole munthu aliyense kunyamula chotengera kupyola pakati pa Kachisi. Ndipo anaphunzitsa, nanena nao, Sichilembedwa kodi, Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yakupempheramo anthu a mitundu yonse? Koma inu mwaiyesa phanga la achifwamba. Ndipo ansembe aakulu ndi alembi anamva, nafunafuna momuonongera Iye; pakuti anamuopa, chifukwa khamu lonse la anthu linazizwa ndi chiphunzitso chake. Ndipo masiku onse madzulo anatuluka Iye m'mudzi. Ndipo m'mene anapitapo m'mawa mwake, anaona kuti mkuyu uja unafota, kuyambira kumizu. Ndipo Petro anakumbukira, nanena naye, Rabi, onani, wafota mkuyuwo munautemberera. Ndipo Yesu anayankha nanena nao, Khulupirirani Mulungu. Ndithu ndinena ndi inu, kuti, Munthu aliyense akanena ndi phiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nyanja; wosakayika mumtima mwake, koma adzakhulupirira kuti chimene achinena chichitidwa, adzakhala nacho. Chifukwa chake ndinena ndi inu, Zinthu zilizonse mukazipemphera ndi kuzipempha, khulupirirani kuti mwazilandira, ndipo mudzakhala nazo. Ndipo pamene muimirira ndi kupemphera, khululukirani, ngati munthu wakulakwirani kanthu; kuti Atate wanunso ali Kumwamba akhululukire inu zolakwa zanu. *** Ndipo iwo anadzanso ku Yerusalemu; ndipo m'mene Iye anali kuyenda m'Kachisi, anafika kwa Iye ansembe aakulu, ndi alembi ndi akulu; nanena naye, Izi muzichita ndi ulamuliro wotani? Kapena anakupatsani ndani ulamuliro uwu wakuchita izi? Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ndikufunsani mau amodzi, mundiyankhe Ine, ndipo ndidzakuuzani ulamuliro umene ndichita nao zinthu zimenezi. Ubatizo wa Yohane uchokera Kumwamba kodi, kapena kwa anthu? Mundiyankhe. Ndipo anatsutsana mwa iwo okha, nanena, Tikati, Kumwamba; adzanena Iye, Ndipo simunakhulupirira iye bwanji? Koma tikati, Kwa anthu, anaopa anthuwo; pakuti onse anamuyesa Yohane mneneri ndithu. Ndipo iwo anamyankha Yesu, ananena nao, Inenso sindikuuzani ulamuliro umene ndichita nao zinthu zimenezi. Ndipo Iye anayamba kulankhula nao m'mafanizo. Munthu analima munda wamphesa, nauzunguniza ndi linga, nakumba moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa olima munda, namuka kwina. Ndipo m'nyengo yake anatuma kapolo kwa olimawo, kuti alandireko kwa olimawo zipatso za m'munda wamphesa. Ndipo iwo anamtenga iye, nampanda, namchotsa wopanda kanthu. Ndipo anatumanso kapolo wina kwa iwo; ndipo ameneyu anamlasa mutu, namchitira zomchititsa manyazi. Ndipo anatuma wina; iyeyu anamupha; ndi ena ambiri; ena anawapanda, ndi ena anawapha. Anamtsalira mmodzi, ndiye mwana wake wokondedwa; potsiriza anamtuma iye kwa iwo, nanena, Adzamchitira ulemu mwana wanga. Koma olima ajawo, ananena mwa iwo okha, Ameneyu ndiye wolowa nyumba; tiyeni timuphe iye, ndipo mundawu udzakhala wathu. Ndipo anamtenga, namupha iye, namtaya kunja kwa munda. Pamenepo mwini munda adzachita chiyani? Adzafika, nadzaononga olimawo, nadzapereka mundawo kwa ena. Kodi simunawerenga ngakhale lembo ili, Mwala umene anaukana omanga nyumba, womwewu unayesedwa mutu wa pangodya: Ichi chinachokera kwa Ambuye, ndipo chili chozizwitsa m'maso mwathu? Ndipo anayesa kumgwira Iye; koma anaopa khamu la anthu, pakuti anazindikira kuti Iye anakamba fanizo ili kuwatsutsa iwo; ndipo anamsiya Iye, nachoka. Ndipo anatuma kwa Iye ena a Afarisi ndi a Aherode, kuti akamkole Iye m'kulankhula kwake. Ndipo pamene anafika, ananena naye, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli woona, ndipo simusamala munthu; pakuti simuyang'ana nkhope ya anthu, koma muphunzitsa njira ya Mulungu moona: Nkuloleka kodi kupereka msonkho kwa Kaisara, kapena iai? Kodi tipereke kapena tisapereke? Koma Iye anadziwa chinyengo chao, nati kwa iwo, Mundiyeseranji? Nditengereni rupiya latheka, kuti ndilione. Ndipo analitenga. Ndipo ananena nao, Chithunzithunzi ichi, ndi chilembo chake zili za yani? Ndipo anati kwa Iye, Za Kaisara, Ndipo Yesu anati kwa iwo, Perekani zake za Kaisara kwa Kaisara, ndi zake za Mulungu kwa Mulungu. Ndipo anazizwa naye kwambiri. Ndipo anadza kwa Iye Asaduki, amene amanena kuti palibe kuuka kwa akufa; ndipo anamfunsa Iye, nanena, Mphunzitsi, Mose anatilembera, kuti, Akafa mbale wake wa munthu, nasiya mkazi, wosasiya mwana, mbale wake atenge mkazi wake, namuukitsire mbale wakeyo mbeu. Analipo abale asanu ndi awiri; woyamba anakwatira mkazi, nafa, wosasiya mbeu; ndipo wachiwiri anamkwatira, nafa, wosasiya mbeu; ndipo wachitatunso anatero momwemo; ndipo asanu ndi awiriwo analibe kusiya mbeu. Potsiriza pake pa onse mkazinso anafa. Pakuuka adzakhala mkazi wa yani wa iwowa? Pakuti asanu ndi awiriwo adamuyesa mkazi wao. Yesu ananena nao, Simusochera nanga mwa ichi, popeza mulibe kudziwa malembo, kapena mphamvu yake ya Mulungu? Pakuti pamene adzauka kwa akufa, sakwatira, kapena sakwatiwa; koma akhala ngati angelo a Kumwamba. Koma za akufa, kuti akaukitsidwa; simunawerenga m'buku la Mose kodi, za chitsambacho, kuti Mulungu anati kwa iye, nanena, Ine Ndine Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo? Sali Mulungu wa akufa, koma wa amoyo: musochera inu ndithu. Ndipo anadza mmodzi wa alembi, namva iwo alikufunsana pamodzi, ndipo pakudziwa kuti anawayankha bwino, anamfunsa Iye, Lamulo la m'tsogolo la onse ndi liti? Yesu anayankha, kuti, La m'tsogolo ndili, Mvera, Israele; Ambuye Mulungu wathu, Ambuye ndiye mmodzi; ndipo uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse. Lachiwiri ndi ili, Uzikonda mnzako monga udzikonda mwini. Palibe lamulo lina lakuposa awa. Ndipo mlembiyo anati kwa Iye, Chabwino, Mphunzitsi, mwanena zoona kuti ndiye mmodzi; ndipo palibe wina, koma Iye: ndipo, kumkonda Iye ndi mtima wonse, ndi nzeru yonse, ndi mphamvu yonse, ndi kukonda mnzake monga adzikonda mwini, ndiko kuposa nsembe zopsereza zamphumphu zonse, ndi nsembe zophedwa. Ndipo pakuona kuti anayankha ndi nzeru, Yesu anati kwa iye, Suli kutali ndi Ufumu wa Mulungu. Ndipo palibe munthu analimbanso mtima kumfunsa Iye kanthu. Ndipo Yesu pamene anaphunzitsa m'Kachisi, anayankha, nanena, Bwanji alembi anena kuti Khristu ndiye mwana wa Davide? Davide mwini yekha anati mwa Mzimu Woyera, Ambuye anati kwa Ambuye wanga, Khala kudzanja langa lamanja, kufikira ndiwaika adani ako popondapo mapazi ako. Davide mwini yekha amtchula Iye Ambuye; ndipo ali mwana wake bwanji? Ndipo anthu a makamuwo anakondwa kumva Iye. Ndipo m'chiphunzitso chake ananena, Yang'anirani mupewe alembi, akufuna kuyendayenda ovala miinjiro, ndi kulonjeredwa pamisika, ndi kukhala nayo mipando yaulemu m'sunagoge, ndi malo aulemu pamaphwando: amenewo alusira nyumba za akazi amasiye, napemphera monyenga mau ambiri; amenewa adzalandira kulanga koposa. Ndipo Iye anakhala pansi pandunji pa mosungiramo ndalama, napenya kuti khamu la anthu alikuponya ndalama mosungiramo; ndipo eni chuma ambiri anaponyamo zambiri. Ndipo anadza mkazi wamasiye waumphawi, ndipo iye anaponyamo tindalama tiwiri tating'ono tokwanira kakobiri kamodzi. Ndipo anaitana ophunzira ake, nati kwa iwo, Ndithu ndinena ndi inu, Mkazi wamasiye amene waumphawi anaponya zambiri koposa onse akuponya mosungiramo: pakuti anaponyamo onse mwa zochuluka zao; koma iye anaponya mwa kusowa kwake zonse anali nazo, inde moyo wake wonse. Ndipo pamene analikutuluka Iye m'Kachisi, mmodzi wa ophunzira ake ananena kwa Iye, Mphunzitsi, onani, miyala yotere ndi nyumba yotere. Ndipo Yesu anati kwa iye, Kodi waona nyumba izi zazikulu? Sudzasiyidwa pano mwala umodzi pamwamba pa unzake, umene sudzagwetsedwa. Ndipo pamene anakhala Iye pa phiri la Azitona, popenyana ndi Kachisi, anamfunsa Iye m'tseri Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, ndi Andrea, kuti, Tiuzeni, zinthu izi zidzachitika liti? Ndi chotani chizindikiro chake chakuti zili pafupi pa kumalizidwa zinthu izi zonse? Ndipo Yesu anayamba kunena nao, Yang'anirani kuti munthu asakusocheretseni. Ambiri adzafika m'dzina langa, nadzanena, Ine ndine Iye; nadzasocheretsa ambiri. Ndipo m'mene mudzamva za nkhondo ndi mbiri zake za nkhondo, musamadera nkhawa: ziyenera kuchitika izi; koma sichinafike chimaliziro. Pakuti mtundu wa anthu udzayambana ndi mtundu wina, ndipo ufumu ndi ufumu unzake: padzakhala zivomezi m'malo m'malo; padzakhala njala; izi ndi zoyambira za zowawa. Koma inu mudziyang'anire inu nokha; pakuti adzakuperekani inu kwa akulu a milandu; ndipo adzakukwapulani m'masunagoge; ndipo pamaso pa akazembe ndi mafumu mudzaimirira chifukwa cha Ine, kukhale umboni kwa iwo. Ndipo Uthenga Wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse. Ndipo pamene adzapita nanu kumlandu, nadzakuperekani, musade nkhawa usanayambe mlandu ndi chimene mudzalankhula; koma chimene chidzapatsidwa kwa inu m'mphindi yomweyo, muchilankhule; pakuti olankhula si ndinu, koma Mzimu Woyera. Ndipo mbale adzapereka mbale wake kuti amuphe, ndi atate mwana wake; ndi ana adzayambana ndi akuwabala, nadzawaphetsa. Ndipo adzada inu anthu onse chifukwa cha dzina langa: koma iye wakupirira kufikira chimaliziro, yemweyo adzapulumutsidwa. Ndipo pamene mukaona chonyansa cha kupululutsa chilikuima pomwe sichiyenera (wakuwerenga azindikire), pamenepo a m'Yudeya athawire kumapiri: ndi iye amene ali pamwamba pa chindwi asatsike, kapena asalowe kukatulutsa kanthu m'nyumba mwake; ndi iye amene ali kumunda asabwere kudzatenga malaya ake. Koma tsoka iwo akukhala ndi pakati, ndi akuyamwitsa ana masiku awo! Ndipo pempherani kuti kusakhale m'nyengo yachisanu. Pakuti masiku aja padzakhala chisautso, chonga sichinakhala chinzake kuyambira chiyambi cha chilengedwe chimene Mulungu anachilenga ndi kufikira tsopano, ndipo sichidzakhalanso, nthawi zonse. Ndipo Ambuye akadapanda kufupikitsa masikuwo, sakadapulumuka munthu mmodzi yense; koma chifukwa cha osankhidwa amene anawasankha, anafupikitsa masikuwo. Ndipo pamenepo wina akati kwa inu, Onani Khristu ali pano; kapena, Onani, uko; musavomereze; pakuti adzauka Akhristu onyenga ndi aneneri onyenga, ndipo adzachita zizindikiro ndi zozizwitsa, kuti akasocheretse, ngati nkutheka, osankhidwa omwe. Koma yang'anirani; onani ndakuuziranitu zinthu zonse, zisanafike. Koma m'masikuwo, chitatha chisautso chimenecho, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzapatsa kuunika kwake, ndi nyenyezi zidzagwa kuchokera m'mwamba ndi mphamvu zili m'mwamba zidzagwedezeka. Ndipo pamenepo adzaona Mwana wa Munthu alinkudza m'mitambo ndi mphamvu yaikulu, ndi ulemerero. Ndipo pamenepo adzatuma angelo, nadzasonkhanitsa osankhidwa ake ochokera kumphepo zinai, kuyambira ku malekezero ake a dziko lapansi, ndi kufikira ku malekezero a thambo. Ndipo phunzirani ndi mkuyu fanizo lake; pamene pafika kuti nthambi yake ikhala yanthete, ndipo anaphuka masamba ake, muzindikira kuti layandikira dzinja; chomwecho inunso, pamene muona zinthu izi zilikuchitika, zindikirani kuti ali pafupi pakhomo. Indetu ndinena ndi inu, Mbadwo uno sudzapita kufikira zinthu izi zonse zitachitika. Thambo ndi dziko lapansi zidzapita; koma mau anga sadzapita. Koma za tsiku ilo, kapena nthawi yake sadziwa munthu, angakhale angelo m'Mwamba, angakhale Mwana, koma Atate ndiye. Yang'anirani, dikirani, pempherani: pakuti simudziwa nthawi yake. Monga ngati munthu wa paulendo, adachoka kunyumba kwake, nawapatsa akapolo ake ulamuliro, kwa munthu aliyense ntchito yake, nalamula wapakhomo adikire. Chifukwa chake dikirani; pakuti simudziwa inu nthawi yake yakubwera mwini nyumba, kapena madzulo, kapena pakati pausiku, kapena pakulira tambala, kapena mamawa; kuti angabwere balamanthu nakakupezani muli m'tulo. Ndipo chimene ndinena ndi inu ndinena kwa onse, Dikirani. Ndipo popita masiku awiri kuli phwando la Paska ndi mikate yopanda chotupitsa; ndipo ansembe aakulu ndi alembi anafunafuna momchitira chiwembu, ndi kumupha: pakuti anati, Pachikondwerero ai, kuti pangakhale phokoso la anthu. Ndipo pakukhala Iye ku Betaniya m'nyumba ya Simoni wakhate, m'mene anaseama kudya, anadzapo mkazi ali nayo nsupa ya alabastero ya mafuta onunkhira bwino a narido weniweni a mtengo wapatali; naswa nsupayo, nawatsanulira pamutu pake. Koma anakhalako ena anavutika mtima mwa iwo okha, ndi kuti, Mafutawo atayidwa chifukwa ninji? Pakuti mafuta amene akadagula marupiya atheka mazana atatu ndi mphamvu zake, ndi kupatsa aumphawi. Ndipo anadandaulira mkaziyo. Koma Yesu anati, Mlekeni, mumvutiranji? Wandichitira Ine ntchito yabwino. Pakuti muli nao aumphawi pamodzi ndi inu masiku onse, ndipo paliponse pamene mukafuna mukhoza kuwachitira zabwino; koma Ine simuli nane masiku onse. Iye wachita chimene wakhoza; anandidzozeratu thupi langa ku kuikidwa m'manda. Ndipo ndithu ndinena ndi inu, Ponse pamene padzalalikidwa Uthenga Wabwino kudziko lonse lapansi, ichinso chimene anachita mkazi uyu chidzanenedwa, chikhale chonkumbukira nacho. Ndipo Yudasi Iskariote, ndiye mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anachoka napita kwa ansembe aakulu, kuti akampereke Iye kwa iwo. Ndipo pamene iwo anamva, anasekera, nalonjezana naye kuti adzampatsa ndalama. Ndipo iye anafunafuna pompereka Iye bwino. Ndipo tsiku loyamba la mikate yopanda chotupitsa, pamene amapha Paska, ophunzira ananena naye, Mufuna tinke kuti, tikakonze mkadyereko Paska? Ndipo anatuma awiri a ophunzira ake, nanena nao, Lowani m'mzinda, ndipo adzakomana nanu munthu wakusenza mtsuko wa madzi; mumtsate iye; ndipo kumene akalowako iye, munene naye mwini nyumba, Mphunzitsi anena, Chilikuti chipinda cha alendo changa, m'menemo ndikadye Paska ndi ophunzira anga? Ndipo iye yekha adzakusonyezani chipinda chapamwamba chachikulu choyalamo ndi chokonzedwa; ndipo m'menemo mutikonzere. Ndipo ophunzira anatuluka, nafika m'mzinda, napeza monga anati kwa iwo; ndipo anakonza Paska. Ndipo pofika madzulo anadza Iye pamodzi ndi khumi ndi awiriwo. Ndipo pamene anaseama iwo kudya, Yesu anati, Ndithu ndinena ndi inu, Mmodzi wa inu adzandipereka Ine, ndiye wakudya ndi Ine pamodzi. Anayamba iwo kukhala ndi chisoni, ndi kunena naye mmodzimmodzi, kuti, Ndine kodi? Ndipo anati kwa iwo, Mmodzi wa khumi ndi awiriwo, ndiye wakusunsa pamodzi ndi Ine m'mbale. Pakuti Mwana wa Munthu amukadi, monga kwalembedwa za Iye; koma tsoka munthuyo amene apereka Mwana wa Munthu! Kukadakhala bwino kwa munthu ameneyo ngati sakadabadwa iye. Ndipo pamene iwo analikudya, Iye anatenga mkate, ndipo pamene anadalitsa, ananyema, napereka kwa iwo, kuti, Tengani; thupi langa ndi ili. Ndipo anatenga chikho, ndipo pamene adayamika, anapereka kwa iwo; ndipo iwo onse anamweramo. Ndipo Iye anati kwa iwo, Ichi ndi mwazi wanga wa chipangano, wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri. Ndipo ndinena nanu, Sindidzamwanso chipatso cha mpesa, kufikira tsiku lijalo, limene ndidzamwa icho chatsopano mu Ufumu wa Mulungu. Ndipo ataimba nyimbo, anatuluka, namuka kuphiri la Azitona. Ndipo Yesu ananena nao, Mudzakhumudwa nonsenu; pakuti kwalembedwa, Ndidzakantha mbusa, ndi nkhosa zidzamwazika. Komatu nditadzauka ndidzatsogolera inu ku Galileya. Koma Petro ananena naye, Angakhale adzakhumudwa onse, komatu ine iai. Ndipo Yesu ananena naye, Ndithu ndinena ndi iwe, kuti lero, usiku uno, tambala asanalire kawiri, udzandikana Ine katatu. Koma iye analimbitsa mau chilimbitsire, kuti, Ngakhale ndidzafa nanu, sindidzakana Inu. Ndipo onsewo anatero. Ndipo iwo anadza kumalo dzina lake Getsemani; ndipo ananena kwa ophunzira ake, Bakhalani pano, kufikira ndikapemphera. Ndipo anatenga pamodzi ndi Iye Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, nayamba kudabwa kwambiri, ndi kusauka mtima ndithu. Ndipo ananena nao, Moyo wanga uli wa chisoni chambiri, kufikira imfa. Bakhalani pano, nimundikire. Ndipo Iye anapita m'tsogolo pang'ono, nagwa pansi, napemphera kuti ngati nkutheka nthawi imene impitirire. Ndipo ananena, Abba, Atate, zinthu zonse zitheka ndi Inu; mundichotsere chikho ichi; komatu si chimene ndifuna Ine, koma chimene mufuna Inu. Ndipo anadza nawapeza iwo ali m'tulo, nanena ndi Petro, Simoni, ugona kodi? Unalibe mphamvu yakudikira ora limodzi kodi? Dikirani, pempherani, kuti mungalowe m'kuyesedwa; mzimutu uli wakufuna, koma thupi lili lolefuka. Ndipo anachokanso, napemphera, nanena mau omwewo. Ndipo anadzanso nawapeza ali m'tulo, pakuti maso ao analemeradi; ndipo sanadziwe chomyankha Iye. Ndipo anadza kachitatu, nanena nao, Gonani tsopano, nimupumule; chakwanira; yafika nthawi; onani Mwana wa Munthu aperekedwa m'manja a anthu ochimwa. Ukani, tizimuka; onani wakundiperekayo ali pafupi. Ndipo pomwepo, Iye ali chilankhulire, anadza Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, ndipo pamodzi naye khamu la anthu, ali nao malupanga ndi mikunkhu, ochokera kwa ansembe aakulu ndi alembi ndi akulu. Ndipo wakumpereka Iye anawapatsa chizindikiro, nanena, Iye amene ndidzampsompsona, ndiyetu; mgwireni munke naye chisungire. Ndipo atafika, pomwepo anadza kwa Iye, nanena, Rabi; nampsompsonetsa. Ndipo anamthira manja, namgwira. Koma mmodzi wina wa iwo akuimirirapo, anasolola lupanga lake, nakantha kapolo wake wa mkulu wa ansembe, namdula khutu lake. Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Kodi mwatuluka ndi malupanga ndi mikunkhu kundigwira Ine monga wachifwamba? Masiku onse ndinali nanu m'Kachisi ndilikuphunzitsa, ndipo simunandigwira Ine; koma ichi chachitika kuti malembo akwanitsidwe. Ndipo iwo onse anamsiya Iye, nathawa. Ndipo mnyamata wina anamtsata Iye, atafundira pathupi bafuta yekha; ndipo anamgwira; koma iye anasiya bafutayo, nathawa wamaliseche. Ndipo ananka naye Yesu kwa mkulu wa ansembe; ndipo anasonkhana kwa iye ansembe aakulu onse ndi akulu a anthu, ndi alembi. Ndipo Petro adamtsata Iye kutali, kufikira kulowa m'bwalo la mkulu wa ansembe; ndipo anali kukhala pansi pamodzi ndi anyamata, ndi kuotha moto. Ndipo ansembe aakulu ndi akulu a milandu onse anafunafuna umboni wakutsutsa nao Yesu kuti amuphe Iye; koma sanaupeze. Pakuti ambiri anamchitira umboni wonama, ndipo umboni wao sunalingana. Ndipo ananyamukapo ena, namchitira umboni wakunama, nanena kuti, Ife tinamva Iye alikunena, kuti, Ine ndidzaononga Kachisi uyu wopangidwa ndi manja, ndi masiku atatu ndidzamanga wina wosapangidwa ndi manja. Ndipo ngakhale momwemo umboni wao sunalingana. Ndipo mkulu wa ansembe ananyamuka pakati, namfunsa Yesu, nanena, Suyankha kanthu kodi? Nchiyani ichi chimene awa alikuchitira mboni? Koma anakhala chete, osayankha kanthu. Mkulu wa ansembe anamfunsanso, nanena naye, Kodi Iwe ndiwe Khristu, Mwana wake wa Wolemekezeka? Ndipo Yesu anati, Ndine amene; ndipo mudzaona Mwana wa Munthu alikukhala kudzanja lamanja la mphamvu, ndi kudza ndi mitambo ya kumwamba. Ndipo mkulu wa ansembe anang'amba malaya ake, nanena, Tifuniranjinso mboni zina? Mwamva mwano wake; muyesa bwanji? Ndipo onse anamtsutsa Iye kuti ayenera kufa. Ndipo ena anayamba kumthira malovu Iye, ndi kuphimba nkhope yake, ndi kumbwanyula, ndi kunena naye, Lota; ndipo anyamatawo anampanda Iye khofu. Ndipo pamene Petro anali pansi m'bwalo, anadzapo mmodzi wa adzakazi a mkulu wa ansembe; ndipo anaona Petro alikuotha moto, namyang'ana iye, nanena, Iwenso unali naye Mnazarene, Yesu. Koma anakana, nanena, Sindidziwa kapena kumvetsa chimene uchinena iwe; ndipo anatuluka kunka kuchipata; ndipo tambala analira. Ndipo anamuona mdzakaziyo, nayambanso kunena ndi iwo akuimirirapo, Uyu ngwa awo. Koma anakananso. Ndipo patapita kamphindi, akuimirirapo ananenanso ndi Petro, Zedi uli wa awo; pakutinso uli Mgalileya. Koma iye anayamba kutemberera, ndi kulumbira, Sindimdziwa munthuyu mulikunena. Ndipo pomwepo tambala analira kachiwiri. Ndipo Petro anakumbukira umo Yesu anati kwa iye, kuti, Tambala asanalire kawiri udzandikana katatu. Ndipo pakuganizira ichi analira misozi. Ndipo pomwepo mamawa anakhala upo ansembe aakulu, ndi akulu a anthu, ndi alembi, ndi akulu a milandu onse, namanga Yesu, namtenga, nampereka kwa Pilato. Ndipo Pilato anamfunsa Iye, Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo anayankha, nanena naye, Mwatero. Ndipo ansembe aakulu anamnenera Iye zinthu zambiri. Ndipo Pilato anamfunsanso, nanena, Suyankha kanthu kodi? Taona, akunenera Iwe zinthu zambiri zotere. Koma Yesu sanayankhenso kanthu; kotero kuti Pilato anazizwa. Ndipo ankawamasulira pachikondwerero wandende mmodzi, amene iwo anampempha. Ndipo analipo wina dzina lake Barabasi, wamangidwa pamodzi ndi opanduka, amene anapha munthu mumphandumo. Ndipo khamu la anthu anabwera nayamba kupempha kuti achite monga anali kuwachitira nthawi zonse. Ndipo Pilato anawayankha, nanena nao, Kodi mufuna kuti ndikumasulireni mfumu ya Ayuda? Pakuti anazindikira kuti ansembe aakulu anampereka Iye mwanjiru. Koma ansembe aakulu anasonkhezera khamulo, kuti makamaka awamasulire Barabasi. Ndipo Pilato anawayankhanso, nati kwa iwo, Pamenepo ndidzachita chiyani ndi Iye amene mumtchula mfumu ya Ayuda? Ndipo anafuulanso, Mpachikeni pamtanda. Ndipo Pilato ananena nao, Pakuti Iye anachita choipa chotani? Koma iwo anafuulitsatu, Mpachikeni Iye. Ndipo Pilato pofuna kuwakhazika mtima anthuwo, anawamasulira Barabasi, napereka Yesu, atamkwapula, akampachike pamtanda. Ndipo asilikali anachoka naye nalowa m'bwalo, ndilo Pretorio; nasonkhanitsa gulu lao lonse. Ndipo anamveka Iye chibakuwa, naluka korona waminga, namveka pa Iye; Ndipo anayamba kumlankhula Iye, kuti, Tikuoneni, mfumu ya Ayuda! Ndipo anampanda Iye pamutu pake ndi bango, namthira malovu, nampindira maondo, namlambira. Ndipo atatha kumnyoza anamvula chibakuwacho namveka Iye zovala zake. Ndipo anatuluka naye kuti akampachike Iye pamtanda. Ndipo anakakamiza wina wopitirirapo, Simoni wa ku Kirene, alikuchokera kuminda, atate wao wa Aleksandro ndi Rufu, kuti anyamule mtanda wake. Ndipo anamtenga kunka naye kumalo Gologota, ndiwo, osandulika, Malo a Bade. Ndipo anampatsa vinyo wosanganiza ndi mure; koma Iye sanamlandire. Ndipo anampachika Iye, nagawana zovala zake mwa iwo okha, ndi kuchita maere pa izo, kuti adziwe yense adzatenga chiyani. Ndipo panali ora lachitatu, ndipo anampachika Iye. Ndipo lembo la mlandu wake linalembedwa pamwamba, MFUMU YA AYUDA. Ndipo anapachika pamodzi ndi Iye achifwamba awiri; mmodzi kudzanja lake lamanja ndi wina kulamanzere. *** Ndipo iwo akupitirirapo anamchitira mwano, napukusa mitu yao, nanena, Ha! Iwe wakupasula Kachisi, ndi kummanga masiku atatu, udzipulumutse mwini, nutsike pamtanda. Moteronso ansembe aakulu anamtonza mwa iwo okha pamodzi ndi alembi, nanena, Anapulumutsa ena; sakhoza kudzipulumutsa yekha. Atsike tsopano pamtanda, Khristu mfumu ya Israele, kuti tione, ndi kukhulupirira. Ndipo iwo akupachikidwa naye anamlalatira. Ndipo pofika ora lachisanu ndi chimodzi, panali mdima pa dziko lonse, kufikira ora lachisanu ndi chinai. Ndipo pa ora lachisanu ndi chinai Yesu anafuula ndi mau okweza, Eloi, Eloi, lama sabakitani? ndiko kusandulika, Mulungu wanga, Mulungu wanga mwandisiyiranji Ine? Ndipo ena akuimirirapo, pakumva, ananena, Taonani, aitana Eliya. Ndipo anathamanga wina, nadzaza chinkhupule ndi vinyo wosasa, nachiika pabango, namwetsa Iye, nanena, Lekani; tione ngati Eliya adza kudzamtsitsa. Ndipo Yesu anatulutsa mau okweza, napereka mzimu wake. Ndipo chinsalu chotchinga cha m'Kachisi chinang'ambika pakati, kuyambira kumwamba kufikira pansi. Ndipo pamene kenturiyo, woimirirapo popenyana ndi Iye, anaona kuti anapereka mzimu kotero, anati, Zoonadi, munthu uyu anali Mwana wa Mulungu. Ndipo analinso kumeneko akazi akuyang'anira kutali; mwa iwo anali Maria wa Magadala, ndi Maria amake wa Yakobo wamng'ono ndi wa Yosefe, ndi Salome; amene anamtsata Iye, pamene anali m'Galileya, namtumikira; ndi akazi ena ambiri, amene anakwera kudza ndi Iye ku Yerusalemu. Ndipo atafika tsono madzulo, popeza mpa tsiku lokonzekera, ndilo la pambuyo pa Sabata, anadzapo Yosefe wa ku Arimatea, mkulu wa milandu womveka, amene yekha analikuyembekezera Ufumu wa Mulungu; nalimba mtima nalowa kwa Pilato, napempha mtembo wake wa Yesu. Ndipo Pilato anazizwa ngati adamwaliradi; naitana kenturiyo, namfunsa ngati adamwalira kale. Ndipo pamene anachidziwa ndi kenturiyo, anamninkha Yosefe mtembowo. Ndipo anagula bafuta, namtsitsa Iye, namkulunga m'bafutamo, namuika m'manda osemedwa m'thanthwe; nakunkhunizira mwala pakhomo la manda. Ndipo Maria wa Magadala ndi Maria amake wa Yosefe anapenya pomwe anaikidwapo. Ndipo litapita Sabata, Maria wa Magadala, ndi Maria amake wa Yakobo, ndi Salome, anagula zonunkhira, kuti akadze kumdzoza Iye. Ndipo anadza kumanda mamawa tsiku loyamba la Sabata, litatuluka dzuwa. Ndipo analikunena mwa okha, Adzatikunkhunizira ndani mwalawo, pakhomo la manda? Ndipo pamene anakweza maso anaona kuti mwala wakunkhunizidwa, pakuti unali waukulu ndithu. Ndipo pamene analowa m'manda, anaona mnyamata alikukhala kumbali ya kudzanja lamanja, wovala mwinjiro woyera; ndipo iwo anadabwa. Ndipo iye ananena nao, Musadabwe: mulikufuna Yesu Mnazarene amene anapachikidwa; anauka; sali pano; taonani, mbuto m'mene anaikamo Iye! Koma mukani, uzani ophunzira ake, ndi Petro, kuti akutsogolerani inu ku Galileya; kumeneko mudzamuona Iye, monga ananena ndi inu. Ndipo anatuluka iwo, nathawa kumanda; pakuti kunthunthumira ndi kudabwa kwakukulu kudawagwira; ndipo sanauze kanthu kwa munthu aliyense; pakuti anachita mantha. Ndipo pamene Iye adauka mamawa tsiku loyamba la sabata, anayamba kuonekera kwa Maria wa Magadala, amene Iye adamtulutsira ziwanda zisanu ndi ziwiri. Iyeyu anapita kuwauza iwo amene ankakhala naye, ali ndi chisoni ndi kulira misozi. Ndipo iwowo, pamene anamva kuti ali moyo, ndi kuti adapenyeka kwa iye, sanamvere. Ndipo zitatha izi, anaonekanso Iye m'maonekedwe ena kwa awiri a iwo alikuyenda kupita kumilaga. Ndipo iwowa anachoka nawauza otsala; koma iwo omwe sanawavomereze. Ndipo chitatha icho anaonekera kwa khumi ndi mmodzi iwo okha, alikuseama pachakudya; ndipo anawadzudzula chifukwa cha kusavomereza kwao ndi kuuma mtima, popeza sanavomereza iwo amene adamuona, atauka Iye. Ndipo ananena nao, Mukani kudziko lonse lapansi, lalikirani Uthenga Wabwino kwa olengedwa onse. Amene akhulupirira nabatizidwa, adzapulumutsidwa; koma amene sakhulupirira adzalangidwa. Ndipo zizindikiro izi zidzawatsata iwo akukhulupirira: m'dzina langa adzatulutsa ziwanda; adzalankhula ndi malankhulidwe atsopano; adzatola njoka, ndipo ngakhale akamwa kanthu kakufa nako, sikadzawapweteka; adzaika manja ao pa odwala, ndipo adzachira. Pamenepo Ambuye Yesu, atatha kulankhula nao, analandiridwa Kumwamba, nakhala pa dzanja lamanja la Mulungu. Ndipo iwowa anatuluka, nalalikira ponseponse, ndipo Ambuye anachita nao pamodzi, natsimikiza mau ndi zizindikiro zakutsatapo. Amen. Popeza ambiri anayesa kulongosola nkhani ya zinthu zinachitika pakati pa ife, monga anazipereka kwa ife iwo amene anakhala mboni ndi atumiki a mau, kuyambira pachiyambi, ndinayesa nkokoma inenso, amene ndinalondalonda mosamalitsa zinthu zonse kuyambira pachiyambi, kulembera kwa iwe tsatanetsatane, Teofilo wabwinotu iwe; kuti udziwitse zoona zake za mau amene unaphunzira. Masiku a Herode, mfumu ya Yudeya, kunali munthu wansembe, dzina lake Zekariya, wa gulu la ansembe la Abiya; ndi mkazi wake wa ana akazi a fuko la Aroni, dzina lake Elizabeti. Ndipo onse awiri anali olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m'malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osachimwa. Ndipo analibe mwana, popeza Elizabeti anali wouma, ndipo onse awiri anakalamba. Ndipo panali, pakuchita iye ntchito yakupereka nsembe m'dongosolo la gulu lake, pamaso pa Mulungu, monga mwa machitidwe a kupereka nsembe, adamgwera maere akufukiza zonunkhira polowa iye m'Kachisi wa Ambuye. Ndipo khamu lonse la anthu linalikupemphera kunja nthawi ya zonunkhira. Ndipo anamuonekera iye mngelo wa Ambuye, naimirira kudzanja lamanja la guwa la nsembe la zonunkhira. Ndipo Zekariya anadabwa pamene anamuona, ndipo mantha anamgwira. Koma mngelo anati kwa iye, Usaope Zekariya, chifukwa kuti lamveka pemphero lako, ndipo mkazi wako Elizabeti adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yohane. Ndipo udzakhala nako kukondwera ndi msangalalo; ndipo anthu ambiri adzakondwera pa kubadwa kwake. Pakuti iye adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye, ndipo sadzamwa konse vinyo kapena kachasu; nadzadzazidwa ndi Mzimu Woyera, kuyambira asanabadwe. Ndipo iye adzatembenuzira ana a Israele ambiri kwa Ambuye Mulungu wao. Ndipo adzamtsogolera Iye, ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kutembenuzira mitima ya atate kwa ana ao, ndi osamvera kuti atsate nzeru ya olungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu okonzeka. Ndipo Zekariya anati kwa mngelo, Ndidzadziwitsa ichi ndi chiyani? Pakuti ndine nkhalamba, ndipo zaka zake za mkazi wanga zachuluka. Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Ine ndine Gabriele, woimirira pamaso pa Mulungu; ndipo ndinatumidwa kwa iwe kudzalankhula nawe, ndi kuuza iwe uthenga uwu wabwino. Ndipo taona, udzakhala wotonthola ndi wosakhoza kulankhula, kufikira tsiku limene zidzachitika izi, popeza kuti sunakhulupirira mau anga, amene adzakwanitsidwa pa nyengo yake. Ndipo anthu analikulindira Zekariya, nazizwa ndi kuchedwa kwake m'Kachisimo. Koma m'mene iye anatulukamo, sanatha kulankhula nao; ndipo anazindikira kuti iye adaona masomphenya m'Kachisimo. Ndipo iye analinkukodola iwo, nakhalabe wosalankhula. Ndipo kunali, pamene masiku a utumiki wake anamalizidwa, anamuka kunyumba kwake. Ndipo atatha masiku awa, Elizabeti mkazi wake anaima; nadzibisa miyezi isanu, nati, Ambuye wandichitira chotero m'masiku omwe Iye anandipenyera, kuchotsa manyazi anga pakati pa anthu. Ndipo mwezi wachisanu ndi chimodzi mngelo Gabriele anatumidwa ndi Mulungu kunka kumudzi wa ku Galileya dzina lake Nazarete, kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, dzina lake Yosefe, wa fuko la Davide; ndipo dzina lake la namwaliyo ndilo Maria. Ndipo pakulowa mngelo anati kwa iye, Tikuoneni, wochitidwa chisomo, Ambuye ali ndi iwe. Koma iye ananthunthumira ndi mau awa, nasinkhasinkha kulonjera uku nkutani. Ndipo mngelo anati kwa iye, Usaope, Maria; pakuti wapeza chisomo ndi Mulungu. Ndipo taona, udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wamwamuna, nudzamutcha dzina lake Yesu. Iye adzakhala wamkulu, nadzatchedwa Mwana wa Wamkulukulu: ndipo Ambuye Mulungu adzampatsa Iye mpando wachifumu wa Davide atate wake: ndipo Iye adzachita ufumu pa banja la Yakobo kunthawi zonse; ndipo ufumu wake sudzatha. Koma Maria anati kwa mngelo, Ichi chidzachitika bwanji, popeza ine sindidziwa mwamuna? Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe: chifukwa chakenso Choyeracho chikadzabadwa, chidzatchedwa Mwana wa Mulungu. Ndipo taona, Elizabeti mbale wako, iyenso ali ndi pakati pa mwana wamwamuna m'ukalamba wake; ndipo mwezi uno uli wachisanu ndi chimodzi wa iye amene ananenedwa wouma. Chifukwa palibe mau amodzi akuchokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu. Ndipo Maria anati, Onani, mdzakazi wa Ambuye; kukhale kwa ine monga mwa mau anu. Ndipo mngelo anachoka kwa iye. Ndipo Maria ananyamuka masiku amenewa, namuka ndi changu kudziko la mapiri kumudzi wa Yuda; nalowa m'nyumba ya Zekariya, nalonjera Elizabeti. Ndipo panali pamene Elizabeti anamva kulonjera kwake kwa Maria, mwana wosabadwayo anatsalima m'mimba mwake; ndipo Elizabeti anadzazidwa ndi Mzimu Woyera; nakweza mau ndi mfuu waukulu, nati, Wodalitsika iwe mwa akazi, ndipo chodalitsika chipatso cha mimba yako. Ndipo ichi chichokera kuti kudza kwa ine, kuti adze kwa ine amake wa Ambuye wanga? Pakuti ona, pamene mau a moni wako analowa m'makutu anga, mwana anatsalima ndi msangalalo m'mimba mwanga. Ndipo wodala ali iye amene anakhulupirira; chifukwa zidzachitidwa zinthu zimene Ambuye analankhula naye. Ndipo Maria anati, Moyo wanga ulemekeza Ambuye, ndipo mzimu wanga wakondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga, chifukwa Iye anayang'anira umphawi wa mdzakazi wake; pakuti taonani, kuyambira tsopano, anthu a mibadwo yonse adzanditchula ine wodala. Chifukwa Iye Wamphamvuyo anandichitira ine zazikulu; ndipo dzina lake lili loyera. Ndipo chifundo chake chifikira anthu a mibadwomibadwo pa iwo amene amuopa Iye. Iye anachita zamphamvu ndi mkono wake; Iye anabalalitsa odzitama ndi mlingaliro wa mtima wao. Iye anatsitsa mafumu pa mipando yao yachifumu, ndipo anakweza aumphawi. Anawakhutitsa anjala ndi zinthu zabwino, ndipo eni chuma anawachotsa opanda kanthu. Anathangatira Israele mnyamata wake, kuti akakumbukire chifundo, (Monga analankhula kwa makolo athu) kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake kunthawi yonse. Ndipo Maria anakhala ndi iye ngati miyezi itatu, nabweranso kunyumba kwake. Ndipo inakwanira nthawi ya Elizabeti, ya kubala kwake, ndipo anabala mwana wamwamuna. Ndipo anansi ake ndi abale ake anamva kuti Ambuye anakulitsa chifundo chake pa iye; nakondwera naye pamodzi. Ndipo panali tsiku lachisanu ndi chitatu iwo anadza kudzadula kamwanako; ndipo akati amutche dzina la atate wake Zekariya. Ndipo amake anayankha, kuti, Iai; koma adzatchedwa Yohane. Ndipo iwo anati kwa iye, Palibe wina wa abale ako amene atchedwa dzina ili. Ndipo anakodola atate wake, afuna amutche dzina liti? Ndipo iye anafunsa cholemberapo, nalemba, kuti, Dzina lake ndi Yohane. Ndipo anazizwa onse. Ndipo pomwepo panatseguka pakamwa pake, ndi lilime lake linamasuka, ndipo iye analankhula, nalemekeza Mulungu. Ndipo panagwa mantha pa iwo onse akukhala oyandikana nao; ndipo analankhulalankhula nkhani izi zonse m'dziko lonse la mapiri a Yudeya. Ndipo onse amene anazimva anazisunga m'mtima mwao, nanena, Nanga mwana uyu adzakhala wotani? Pakuti dzanja la Ambuye linakhala pamodzi ndi iye. Ndipo atate wake Zekariya anadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nanenera za Mulungu, nati, Wolemekezeka Ambuye, Mulungu wa Israele; chifukwa Iye anayang'ana, nachitira anthu ake chiombolo. Ndipo Iye anatikwezera ife nyanga ya chipulumutso, mwa fuko la Davide mwana wake. Monga Iye analankhula ndi m'kamwa mwa aneneri ake oyera mtima, akale lomwe, chipulumutso cha adani athu, ndi pa dzanja la anthu onse amene atida ife. Kuchitira atate athu chifundo, ndi kukumbukira pangano lake lopatulika; chilumbiro chimene Iye anachilumbira kwa Abrahamu atate wathu. Kutipatsa ife kuti titalanditsidwa kudzanja la adani athu, tidzamtumikira Iye, opanda mantha, m'chiyero ndi chilungamo pamaso pake, masiku athu onse. Eya, ndipo iwetu kamwanawe, udzanenedwa mneneri wa Wamkulukulu; pakuti udzatsogolera Ambuye, kukonza njira zake. Kuwapatsa anthu ake adziwitse chipulumutso, ndi makhululukidwe a machimo ao, chifukwa cha mtima wachifundo wa Mulungu wathu. M'menemo mbandakucha wa kumwamba udzatichezera ife. Kuwalitsira iwo okhala mumdima ndi mthunzi wa imfa; kulunjikitsa mapazi athu mu njira ya mtendere. Ndipo mwanayo anakula, nalimbika mu mzimu wake, ndipo iye anali m'mapululu, kufikira masiku akudzionetsa yekha kwa Israele. Ndipo kunali masiku aja, kuti lamulo linatuluka kwa Kaisara Augusto kuti dziko lonse lokhalamo anthu lilembedwe; ndiko kulembera koyamba pokhala Kwirinio kazembe wa Siriya. Ndipo onse anamuka kulembedwa, munthu aliyense kumudzi wake. Ndipo Yosefe yemwe anakwera kuchokera ku Galileya, kumudzi wa Nazarete, kunka ku Yudeya, kumudzi wa Davide, dzina lake Betelehemu, chifukwa iye anali wa banja ndi fuko lake la Davide; kukalembedwa iye mwini pamodzi ndi Maria, wopalidwa naye ubwenzi; ndi uyu anali ndi pakati. Ndipo panali pokhala iwo komweko, masiku ake a kubala anakwanira. Ndipo iye anabala mwana wake wamwamuna woyamba; namkulunga Iye m'nsalu, namgoneka modyera ng'ombe, chifukwa kuti anasowa malo m'nyumba ya alendo. Ndipo panali abusa m'dziko lomwelo, okhala kubusa ndi kuyang'anira zoweta zao usiku. Ndipo mngelo wa Ambuye anaimirira pa awo, ndi kuwala kwa Ambuye kunawaunikira kozungulira: ndipo anaopa ndi mantha akulu. Ndipo mngelo anati kwa iwo, Musaope; pakuti onani, ndikuuzani inu uthenga wabwino wa chikondwero chachikulu, chimene chidzakhala kwa anthu onse; pakuti wakubadwirani inu lero, m'mudzi wa Davide, Mpulumutsi, amene ali Khristu Ambuye. Ndipo ichi ndi chizindikiro kwa inu: Mudzapeza mwana wakhanda wokuta ndi nsalu atagona modyera. Ndipo dzidzidzi panali pamodzi ndi mngeloyo ambirimbiri a gulu la Kumwamba, natamanda Mulungu, nanena, Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nao. Ndipo panali, pamene angelo anachokera kwa iwo kunka Kumwamba, abusa anati wina ndi mnzake, Tipitiretu ku Betelehemu, tikaone chinthu ichi chidachitika, chimene Ambuye anatidziwitsira ife. Ndipo iwo anadza ndi changu, napeza Maria, ndi Yosefe, ndi mwana wakhanda atagona modyera. Ndipo iwo, m'mene anaona, anadziwitsa anthu za mau analankhulidwa kwa iwo a mwana uyu. Ndipo anthu onse amene anamva anazizwa ndi zinthu abusa adalankhula nao. Koma Maria anasunga mau awa onse, nawalingalira mumtima mwake. Ndipo abusawo anabwera, nalemekeza ndi kutamanda Mulungu pa zinthu zonse anazimva, naziona, monga kunalankhulidwa kwa iwo. Ndipo pamene panakwanira masiku asanu ndi atatu akumdula Iye, anamutcha dzina lake Yesu, limene anatchula mngeloyo asanalandiridwe Iye m'mimba. Ndipo pamene anakwanira masiku a kukonza kwao, monga mwa chilamulo cha Mose, iwo anakwera naye kunka ku Yerusalemu, kukamsonyeza Iye kwa Ambuye, (monga mwalembedwa m'chilamulo cha Ambuye, kuti mwamuna aliyense wotsegula pa mimba ya amake adzanenedwa wopatulika wa kwa Ambuye) ndi kukapereka nsembe monga mwanenedwa m'chilamulo cha Ambuye, njiwa ziwiri, kapena maunda awiri. Ndipo onani, m'Yerusalemu munali munthu, dzina lake Simeoni; ndipo munthu uyu, wolungama mtima ndi wopemphera, analikulindira matonthozedwe a Israele; ndipo Mzimu Woyera anali pa iye. Ndipo anamuululira Mzimu Woyera kuti sadzaona imfa, kufikira adzaona Khristu wake wa Ambuye. Ndipo iye analowa ku Kachisi ndi Mzimu: ndipo pamene atate ndi amake analowa ndi kamwanako Yesu, kudzamchitira Iye mwambo wa chilamulo, pomwepo iye anamlandira Iye m'manja mwake, nalemekeza Mulungu, nati, Tsopano, Ambuye, monga mwa mau anu aja, lolani ine, kapolo wanu, ndichoke mumtendere; chifukwa maso anga adaona chipulumutso chanu, chimene munakonza pamaso pa anthu onse, kuunika kukhale chivumbulutso cha kwa anthu a mitundu, ndi ulemerero wa anthu anu Israele. Ndipo atate ndi amake anali kuzizwa ndi zinthu zolankhulidwa za Iye. Ndipo Simeoni anawadalitsa, nati kwa Maria amake, Taona, Uyu waikidwa akhale kugwa ndi kunyamuka kwa anthu ambiri mwa Israele; ndipo akhale chizindikiro chakutsutsana nacho; eya, ndipo lupanga lidzakupyoza iwe moyo wako; kuti maganizo a m'mitima yambiri akaululidwe. Ndipo panali Anna, mneneri wamkazi, mwana wa Fanuwele, wa fuko la Asere; amene anali wokalamba ndithu, nakhala ndi mwamuna wake, kuyambira pa unamwali wake, zaka zisanu ndi ziwiri, ndipo anali wamasiye wa kufikira zaka zake makumi asanu ndi atatu mphambu zinai, amene sankachoka ku Kachisi, wotumikira Mulungu ndi kusala kudya ndi kupemphera usiku ndi usana. Ndipo iye anafikako pa nthawi yomweyo, navomerezanso kutama Mulungu, nalankhula za Iye kwa anthu onse akuyembekeza chiombolo cha Yerusalemu. Ndipo pamene iwo anatha zonse monga mwa chilamulo cha Ambuye, anabwera ku Galileya, kumudzi kwao, ku Nazarete. Ndipo mwanayo anakula nalimbika, nalikudzala ndi nzeru; ndi chisomo cha Mulungu chinali pa Iye. Ndipo atate wake ndi amake akamuka chaka ndi chaka ku Yerusalemu ku Paska. Ndipo pamene Iye anakhala ndi zaka zake khumi ndi ziwiri, anakwera iwo monga machitidwe a chikondwerero; ndipo pakumaliza masiku ake, pakubwera iwo, mnyamatayo Yesu anatsala m'mbuyo ku Yerusalemu. Ndipo atate ndi amake sanadziwe; koma iwo anayesa kuti Iye ali m'chipiringu cha ulendo, nayenda ulendo wa tsiku limodzi; ndipo anayamba kumfunafuna Iye mwa abale ao ndi mwa anansi ao; ndipo pamene sanampeze, anabwera ku Yerusalemu, namfunafuna Iye. Ndipo pakupita masiku atatu, anampeza Iye m'Kachisi, analikukhala pakati pa aphunzitsi, namva iwo, nawafunsanso mafunso. Ndipo onse amene anamva Iye anadabwa ndi chidziwitso chake, ndi mayankho ake. Ndipo m'mene anamuona Iye, anadabwa; ndipo amake anati kwa Iye, Mwanawe, wachitiranji ife chotero; taona, atate wako ndi ine tinalikufunafuna Iwe ndi kuda nkhawa. Ndipo Iye anati kwa iwo, Kuli bwanji kuti munalikundifunafuna Ine? Simunadziwa kodi kuti kundiyenera Ine ndikhale m'zake za Atate wanga? Ndipo sanadziwitse mau amene Iye analankhula nao. Ndipo anatsika nao pamodzi nadza ku Nazarete; nawamvera iwo: ndipo amake anasunga zinthu izi zonse mumtima mwake. Ndipo Yesu anakulabe m'nzeru ndi mumsinkhu, ndi m'chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu. Ndipo pa chaka chakhumi ndi chisanu cha ufumu wa Tiberio Kaisara, pokhala Pontio Pilato kazembe wa Yudeya, ndi Herode chiwanga cha Galileya, ndi Filipo mbale wake chiwanga cha dziko la Itureya ndi la Trakoniti, ndi Lisaniasi chiwanga cha Abilene; pa ukulu wansembe wao wa Anasi ndi Kayafa, panadza mau a Mulungu kwa Yohane mwana wa Zekariya m'chipululu. Ndipo iye anadza kudziko lonse la m'mbali mwa Yordani, nalalikira ubatizo wa kulapa mtima kuloza ku chikhululukiro cha machimo; monga mwalembedwa m'buku la Yesaya mneneri, kuti, Mau a wofuula m'chipululu, konzani khwalala la Ambuye, lungamitsani njira zake. Chigwa chilichonse chidzadzazidwa, ndipo phiri lililonse ndi mtunda uliwonse zidzachepsedwa; ndipo zokhota zidzakhala zolungama, ndipo njira za zigoloondo zidzakhala zosalala; ndipo anthu onse adzaona chipulumutso cha Mulungu. Chifukwa chake iye ananena kwa makamuwo a anthu amene anatulukira kukabatizidwa ndi iye, Obadwa a njoka inu, anakulangizani inu ndani kuthawa mkwiyo ulinkudza? Chifukwa chake balani zipatso zakuyenera kulapa mtima, ndipo musayambe kunena mwa inu nokha, Atate wathu tili naye ndiye Abrahamu: pakuti ndinena kwa inu, kuti ali ndi mphamvu Mulungu, mwa miyala iyi, kuukitsira Abrahamu ana. Ndiponso tsopano lino nkhwangwa yaikidwa pa mizu ya mitengo; chotero mtengo uliwonse wosabala chipatso chabwino udulidwa, nuponyedwa pamoto. Ndipo anthu a makamu anamfunsa iye, nanena, Ndipo tsono tizichita chiyani? Koma iye anayankha nanena kwa iwo, Iye amene ali nao malaya awiri apatse kwa iye amene alibe; ndi iye amene ali nazo zakudya achite chomwecho. Ndipo amisonkho omwe anadza kudzabatizidwa, nati kwa iye, Mphunzitsi, ife tizichita chiyani? Koma iye anati kwa iwo, Musakapambe kanthu konse kakuposa chimene anakulamulirani. Ndipo asilikali omwe anamfunsa iye, nati, Nanga ife tizichita chiyani? Ndipo iye anati kwa iwo, Musaopse, musanamize munthu aliyense; khalani okhuta ndi kulipira kwanu. Ndipo pamene anthu anali kuyembekezera, ndipo onse anaganizaganiza m'mitima yao za Yohane, ngati kapena iye ali Khristu; Yohane anayankha, nanena kwa onse, Inetu ndikubatizani inu ndi madzi; koma wakundiposa ine mphamvu alinkudza, amene sindiyenera kumasula lamba la nsapato zake; Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto: amene chouluzira chake chili m'dzanja lake, kuti ayeretse padwale pake, ndi kusonkhanitsa tirigu m'nkhokwe yake; koma mankhusu adzatentha m'moto wosazima. Choteretu iye anauza anthu Uthenga Wabwino ndi kuwadandaulira zinthu zina zambiri. Koma Herode mfumu ija, m'mene Yohane anamdzudzula chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa mbale wake, ndi cha zinthu zonse zoipa Herode anazichita, anaonjeza pa zonsezi ichinso, kuti anatsekera Yohane m'nyumba yandende. Pamene anthu onse anabatizidwa, Yesu nayenso anabatizidwa. Iye anali kupemphera, ndipo kuthambo kunatseguka, ndipo Mzimu Woyera anatsika ndi maonekedwe a thupi lake ngati nkhunda, nadza pa Iye; ndipo munatuluka mau m'thambo, kuti, Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, mwa Iwe ndikondwera. Ndipo Yesuyo, pamene anayamba ntchito yake, anali monga wa zaka makumi atatu, ndiye (monga anthu adamuyesa) mwana wa Yosefe, mwana wa Eli, mwana wa Matati, mwana wa Levi, mwana wa Meliki, mwana wa Yanai, mwana wa Yosefe, mwana wa Matatiasi, mwana wa Amosi, mwana wa Nahumu, mwana wa Hesili, mwana wa Nagai, mwana wa Mahati, mwana wa Matatiasi, mwana wa Semeini, mwana wa Yoseke, mwana wa Yoda, mwana wa Yohanani, mwana wa Resa, mwana wa Zerubabele, mwana wa Sealatiele, mwana wa Neri, mwana wa Meliki, mwana wa Adi, mwana wa Kosamu, mwana wa Elimadama, mwana wa Eri, mwana wa Yose, mwana wa Eliyezere, mwana wa Yorimu, mwana wa Matati, mwana wa Levi, mwana wa Simeoni, mwana wa Yudasi, mwana wa Yosefe, mwana wa Yonamu, mwana wa Eliyakimu, mwana wa Melea, mwana wa Mena, mwana wa Matata, mwana wa Natamu, mwana wa Davide, mwana wa Yese, mwana wa Obede, mwana wa Bowazi, mwana wa Salimoni, mwana wa Nasoni, mwana wa Aminadabu, mwana wa Admini, mwana wa Arini, mwana wa Hezironi, mwana wa Perezi, mwana wa Yuda, mwana wa Yakobo, mwana wa Isaki, mwana wa Abrahamu, mwana wa Tera, mwana wa Nahori, mwana wa Serugi, mwana wa Reu, mwana wa Pelegi, mwana wa Eberi, mwana wa Sela, mwana wa Kainani, mwana wa Arifaksadi, mwana wa Semu, mwana wa Nowa, mwana wa Lameki, mwana wa Metusela, mwana wa Enoki, mwana wa Yaredi, mwana wa Mahalalele, mwana wa Kainani, mwana wa Enosi, mwana wa Seti, mwana wa Adamu, mwana wa Mulungu. Ndipo Yesu, wodzala ndi Mzimu Woyera, anabwera kuchokera ku Yordani, natsogozedwa ndi Mzimu kunka kuchipululu kukayesedwa ndi mdierekezi masiku makumi anai. Ndipo Iye sanadye kanthu masiku awo; ndipo pamene anatha anamva njala. Ndipo mdierekezi anati kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, uzani mwala uwu usanduke mkate. Ndipo Yesu anayankha nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha. Ndipo m'mene anamtsogolera anakwera naye, namuonetsa Iye maufumu onse a dziko lokhalamo anthu, m'kamphindi kakang'ono. Ndipo mdierekezi anati kwa Iye, Ine ndidzapatsa Inu ulamuliro wonse umenewu ndi ulemerero wao: chifukwa unaperekedwa kwa ine; ndipo ndiupatsa kwa iye amene ndifuna. Chifukwa chake ngati Inu mudzagwadira pamaso panga, wonsewo udzakhala wanu. Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti, Ambuye Mulungu wako uzimgwadira, ndipo Iye yekhayekha uzimtumikira. Ndipo anamtsogolera Iye ku Yerusalemu, namuika Iye pamwamba penipeni pa Kachisiyo, nati kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, tadzigwetsani nokha pansi; pakuti kwalembedwa kuti, Adzalamula angelo ake za iwe, kuti akutchinjirize. Ndipo, Pa manja ao adzakunyamula iwe, kuti ungagunde konse phazi lako pamwala. Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwanenedwa, Usamuyese Ambuye Mulungu wako. Ndipo mdierekezi, m'mene adamaliza mayesero onse, analekana naye kufikira nthawi ina. Ndipo Yesu anabwera ndi mphamvu ya Mzimu ku Galileya; ndipo mbiri yake ya Iye inabuka ku dziko lonse loyandikira. Ndipo Iye anaphunzitsa m'masunagoge mwao, nalemekezedwa ndi anthu onse. Ndipo anadza ku Nazarete, kumene analeredwa; ndipo tsiku la Sabata analowa m'sunagoge, monga anazolowera, naimiriramo kuwerenga m'kalata. Ndipo anapereka kwa Iye buku la Yesaya mneneri. Ndipo m'mene Iye adafunyulula bukulo, anapeza pomwe panalembedwa, Mzimu wa Ambuye uli pa Ine, chifukwa chake Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino: anandituma Ine kulalikira am'nsinga mamasulidwe, ndi akhungu kuti apenyanso, kutulutsa ndi ufulu ophwanyika, kulalikira chaka chosankhika cha Ambuye. Ndipo m'mene Iye anapinda bukulo, nalipereka kwa mnyamata, anakhala pansi; ndipo maso ao a anthu onse m'sunagogemo anamyang'anitsa Iye. Ndipo anayamba kunena kwa iwo, kuti, Lero lembo ili lakwanitsidwa m'makutu anu. Ndipo onse anamchitira Iye umboni nazizwa ndi mau a chisomo akutuluka m'kamwa mwake; nanena, Kodi uyu si mwana wa Yosefe? Ndipo anati kwa iwo, Kwenikweni mudzati kwa Ine nkhani iyi, Sing'anga iwe, tadzichiritsa wekha: zonse zija tazimva zinachitidwa ku Kapernao, muzichitenso zomwezo kwanu kuno. Ndipo Iye anati, Indetu, ndinena kwa inu, kuti, Palibe mneneri alandirika kudziko la kwao. Koma zoonadi ndinena kwa inu, kuti, Munali akazi amasiye ambiri m'Israele masiku ake a Eliya, pamene kunatsekedwa kumwamba zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi, pamene panakhala njala yaikulu pa dziko lonselo; ndipo Eliya sanatumidwa kwa mmodzi wa iwo, koma ku Sarepta wa ku Sidoni, kwa mkazi wamasiye. Ndipo munali akhate ambiri m'Israele masiku a Elisa mneneri; ndipo palibe mmodzi wa iwo anakonzedwa, koma Naamani yekha wa ku Siriya. Ndipo onse a m'sunagogemo anadzala ndi mkwiyo pakumva izi; nanyamuka namtulutsira Iye kunja kwa mudziwo, nanka naye pamutu pa phiri pamene panamangidwa mudzi wao, kuti akamponye Iye pansi. Koma Iye anapyola pakati pao, nachokapo. Ndipo Iye anatsika nadza ku Kapernao, ndiwo mudzi wa ku Galileya. Ndipo analikuwaphunzitsa iwo pa Sabata; ndipo anadabwa ndi chiphunzitso chake; chifukwa mau ake anali ndi ulamuliro. Ndipo munali m'sunagoge munthu, wokhala nacho chiwanda chonyansa; nafuula ndi mau olimba, kuti, Ha! Tili ndi chiyani ndi Inu, Yesu wa ku Nazarete? Kodi munadza kutiononga ife? Ndikudziwani Inu muli yani, ndinu Woyera wake wa Mulungu. Ndipo Yesu anamdzudzula iye, nanena, Tonthola, nutuluke mwa iye. Ndipo chiwandacho m'mene chinamgwetsa iye pakati, chinatuluka mwa iye chosamphweteka konse. Ndipo anthu onse anadabwa, nalankhulana wina ndi mnzake, nanena, Mau amenewa ali otani? Chifukwa ndi ulamuliro ndi mphamvu angolamulira mizimu yonyansa, ndipo ingotuluka. Ndipo mbiri yake ya Iye inafalikira kumalo onse a dziko loyandikira. Ndipo Iye ananyamuka kuchokera m'sunagoge, nalowa m'nyumba ya Simoni. Koma momwemo munali mpongozi wake wa Simoni, anagwidwa ndi nthenda yolimba yamalungo; ndipo anampempha Yesu za iye. Ndipo Iye anaimirira, naweramira pa iye, nadzudzula nthendayo; ndipo inamleka iye: ndipo anauka msangatu, nawatumikira. Ndipo pakulowa dzuwa anthu onse amene anali nao odwala ndi nthenda za mitundumitundu, anadza nao kwa Iye; ndipo Iye anaika manja ake pa munthu aliyense wa iwo, nawachiritsa. Ndi ziwanda zomwe zinatuluka mwa ambiri, ndi kufuula, kuti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu. Ndipo Iye anazidzudzula, wosazilola kulankhula, chifukwa zinamdziwa kuti Iye ndiye Khristu. Ndipo kutacha anatuluka Iye nanka kumalo achipululu; ndi makamu a anthu analikumfunafuna Iye, nadza nafika kwa Iye, nayesa kumletsa Iye, kuti asawachokere. Koma anati kwa iwo, Kundiyenera Ine ndilalikire Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu kumidzi yinanso: chifukwa ndinatumidwa kudzatero. Ndipo Iye analikulalikira m'masunagoge a ku Yudeya. Ndipo panali, pakumkanikiza khamu la anthu, kudzamva mau a Mulungu, Iye analikuimirira m'mbali mwa nyanja ya Genesarete; ndipo anaona ngalawa ziwiri zinakhala m'mbali mwa nyanja; koma asodzi a nsomba adatuluka m'menemo, nalikutsuka makoka ao. Ndipo Iye analowa m'ngalawa imodzi, ndiyo yake ya Simoni, nampempha iye akankhe pang'ono. Ndipo anakhala pansi m'menemo, naphunzitsa m'ngalawa makamuwo a anthu. Ndipo pamene Iye analeka kulankhula, anati kwa Simoni, Kankhira kwa kuya, nimuponye makoka anu kukasodza. Ndipo Simoni anayankha, nati, Ambuye, tinagwiritsa ntchito usiku wonse osakola kanthu, koma pa mau anu ndidzaponya makoka. Ndipo pamene anachita ichi, anazinga unyinji waukulu wa nsomba; ndipo makoka ao analinkung'ambika; ndipo anakodola anzao a m'ngalawa yinayo, adze awathangate. Ndipo anadza, nadzaza ngalawa zonse ziwiri, motero kuti zinalinkumira. Koma Simoni Petro, pamene anaona, anagwa pansi pa mabondo ake a Yesu, nanena, Muchoke kwa ine, Ambuye, chifukwa ndine munthu wochimwa. Pakuti chizizwo chidagwira iye, ndi onse amene anali naye, pa kusodzako kwa nsomba zimene anazikola; ndipo chimodzimodzinso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedeo, amene anali anzake a Simoni. Ndipo Yesu anati kwa Simoni, Usaope, kuyambira tsopano udzakhala msodzi wa anthu. Ndipo m'mene iwo anakocheza ngalawa zao pamtunda, anasiya zonse, namtsata Iye. Ndipo panali, pamene Iye anali m'mudzi wina, taona, munthu wodzala ndi khate; ndipo pamene anaona Yesu, anagwa nkhope yake pansi, nampempha Iye, nanena, Ambuye, ngati mufuna mungathe kundikonza. Ndipo Iye anatambalitsa dzanja lake, namkhudza, nanena, Ndifuna, takonzeka. Ndipo pomwepo khate linachoka kwa iye. Ndipo Iye anamuuzitsa, kuti asanene kwa munthu aliyense; koma uchoke, nudzionetse wekha kwa wansembe, nupereke nsembe ya pa chikonzedwe chako, monga adalamulira Mose, kukhale umboni kwa iwo. Koma makamaka mbiri yake ya Iye inabuka: ndipo mipingo yambiri ya anthu inasonkhana kudzamvera, ndi kudzachiritsidwa nthenda zao. Koma Iye anazemba, nanka m'mapululu, nakapemphera. Ndipo panali tsiku limodzi la masiku awo, Iye analikuphunzitsa; ndipo analikukhalapo Afarisi ndi aphunzitsi a malamulo, amene anachokera kumidzi yonse ya ku Galileya, ndi Yudeya ndi Yerusalemu: ndipo mphamvu ya Ambuye inali ndi Iye yakuwachiritsa. Ndipo onani, anthu alikunyamulira pakama munthu wamanjenje; nafunafuna kulowa naye, ndi kumuika pamaso pa Iye. Ndipo posapeza polowa naye, chifukwa cha unyinji wa anthu, anakwera pamwamba pa chindwi, namtsitsira iye poboola pa chindwi ndi kama wake, namfikitsa pakati pomwe pamaso pa Yesu. Ndipo Iye, pakuona chikhulupiriro chao, anati, Munthu iwe, machimo ako akhululukidwa. Ndipo alembi ndi Afarisi anayamba kuyesayesa mumtima mwao, kuti, Ndani Uyu alankhula zomchitira Mulungu mwano? Ndani angathe kukhululukira machimo, koma Mulungu yekha? Koma Yesu anadziwa zoyesayesa zao, nayankha, nati kwa iwo, Muyesayesa bwanji m'mitima yanu? Chapafupi nchiti, kunena, Akhululukidwa kwa iwe machimo ako; kapena kunena, Tauka, nuyende? Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali nayo mphamvu pa dziko lapansi yakukhululukira machimo, (anati Iye kwa wamanjenjeyo), Ndinena kwa iwe, Tauka, nusenze kama wako, numuke kunyumba kwako. Ndipo pomwepo anaimirira pamaso pao, nasenza chimene adagonapo, nachokapo, kunka kunyumba kwake, wakulemekeza Mulungu. Ndipo chizizwo chinagwira anthu onse ndipo analemekeza Mulungu; nadzazidwa ndi mantha, nanena kuti, Lero taona zodabwitsa. Ndipo zitatha izi Iye anatuluka, naona munthu wamsonkho, dzina lake Levi, alikukhala polandirira msonkho, nati kwa iye, Unditsate Ine. Ndipo iye anasiya zonse, nanyamuka, namtsata Iye. Ndipo Levi anamkonzera Iye phwando lalikulu kunyumba kwake; ndipo panali khamu lalikulu la amisonkho, ndi enanso amene analikuseama pachakudya pamodzi nao. Ndipo Afarisi ndi alembi ao anang'ung'udza kwa ophunzira ake, nanena, kuti, Bwanji inu mukudya ndi kumwa pamodzi ndi anthu amisonkho ndi ochimwa? Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Amene ali olimba safuna sing'anga; koma akudwala ndiwo. Sindinadza Ine kuitana olungama, koma ochimwa kuti atembenuke mtima. Ndipo iwo anati kwa Iye, Ophunzira a Yohane amasala kudya kawirikawiri, ndi kuchita mapemphero; chimodzimodzinso iwo a Afarisi; koma anu amangokudya ndi kumwa. Koma Yesu anati kwa iwo, Kodi mungathe kuletsa anyamata a ukwati asadye, pamene mkwati ali nao pamodzi? Koma masiku adzafika; ndipo pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, pamenepo adzasala kudya masiku omwewo. Ndipo Iye ananenanso fanizo kwa iwo, kuti, Palibe munthu ang'amba chigamba cha malaya atsopano, nachiphatika pa malaya akale; chifukwa ngati atero, angong'ambitsa atsopanowo, ndi chigamba cha atsopanowo sichidzayenerana ndi akalewo. Ndipo palibe munthu atsanulira vinyo watsopano m'matumba akale; chifukwa ngati atero, vinyo watsopanoyo adzaphulitsa matumba, ndipo ameneyo adzatayika, ndi matumba adzaonongeka. Koma kuyenera kutsanulira vinyo watsopano m'matumba atsopano. Ndipo palibe munthu atamwa vinyo wakale afuna watsopano; pakuti anena, Wakale ali wokoma. Ndipo kunali tsiku la Sabata, Iye analinkupita pakati pa minda ya tirigu; ndipo ophunzira ake analinkubudula ngala za tirigu, nazifikisa m'manja mwao, nadya. Koma Afarisi ena anati, Muchitiranji chosaloledwa kuchitika tsiku la Sabata? Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Kodi simunawerenganso ngakhale chimene anachita Davide, pamene paja anamva njala, iye ndi iwo anali naye pamodzi; kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, natenga mikate yoonetsera, nadya, napatsanso iwo anali naye pamodzi; imeneyi yosaloledwa kudya ena koma ansembe okha? Ndipo Iye ananena kwa iwo, kuti, Mwana wa Munthu ali Mbuye wa tsiku la Sabata. Ndipo kunali tsiku lina la Sabata, Iye analowa m'sunagoge, naphunzitsa. Ndipo munali munthu momwemo, ndipo dzanja lake lamanja linali lopuwala. Ndipo alembi ndi Afarisi analikumzonda Iye, ngati adzachiritsa tsiku la Sabata; kuti akapeze chomneneza Iye. Koma Iye anadziwa maganizo ao; nati kwa munthuyo wa dzanja lake lopuwala, Nyamuka, nuimirire pakatipo. Ndipo Iye ananyamuka, naimirira. Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ndikufunsani inu, Kodi nkulola tsiku la Sabata, kuchita zabwino, kapena kuchita zoipa? Kupulumutsa moyo, kapena kuuononga? Ndipo pamene anaunguzaunguza pa iwo onse, anati kwa iye, Tansa dzanja lako. Ndipo iye anatero, ndi dzanja lake linabwerera momwe. Koma iwowo anagwidwa misala; nalankhulana wina ndi mnzake kuti amchitire Yesu chiyani. Ndipo kunali masiku awa, Iye anatuluka nanka kuphiri kukapemphera; nachezera usiku wonse m'kupemphera kwa Mulungu. Ndipo kutacha, anaitana ophunzira ake; nasankha mwa iwo khumi ndi awiri, amene anawatchanso dzina lao atumwi: Simoni, amene anamutchanso Petro, ndi Andrea mbale wake, ndi Yakobo, ndi Yohane, ndi Filipo, ndi Bartolomeo, ndi Mateyu, ndi Tomasi, ndi Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Simoni wotchedwa Zelote, ndi Yudasi mwana wa Yakobo, ndi Yudasi Iskariote, amene anali wompereka Iye. Ndipo Iye anatsika nao, naima pachidikha, ndi khamu lalikulu la ophunzira ake, ndi unyinji waukulu wa anthu a ku Yudeya lonse ndi Yerusalemu, ndi a ku mbali ya nyanja ya ku Tiro ndi Sidoni, amene anadza kudzamva Iye ndi kudzachiritsidwa nthenda zao; ndipo ovutidwa ndi mizimu yonyansa anachiritsidwa, ndi khamu lonse lija linafuna kumkhudza Iye; chifukwa munatuluka mphamvu mwa Iye, nichiritsa onsewa. Ndipo Iye anakweza maso ake kwa ophunzira ake, nanena, Odala osauka inu; chifukwa uli wanu ufumu wa Mulungu. Odala inu akumva njala tsopano; chifukwa mudzakhuta. Odala inu akulira tsopano; chifukwa mudzaseka. Odala inu, pamene anthu adzada inu, nadzapatula inu, nadzatonza inu, nadzalitaya dzina lanu monga loipa, chifukwa cha Mwana wa Munthu. Kondwerani tsiku lomweli, tumphani ndi chimwemwe; pakuti onani, mphotho zanu nzazikulu Kumwamba; pakuti makolo ao anawachitira aneneri zonga zomwezo. Koma tsoka inu eni chuma! Chifukwa mwalandira chisangalatso chanu. Tsoka inu okhuta tsopano! Chifukwa mudzamva njala. Tsoka inu, akuseka tsopano! Chifukwa mudzachita maliro ndi kulira misozi. Tsoka inu, pamene anthu onse adzanenera inu zabwino! Pakuti makolo ao anawatero momwemo aneneri onama. Koma ndinena kwa inu akumva, Kondanani nao adani anu; chitirani zabwino iwo akuda inu, dalitsani iwo akutemberera inu, pemphererani iwo akuchitira inu chipongwe. Iye amene akupanda iwe pa tsaya limodzi umpatsenso linzake; ndi iye amene alanda chofunda chako, usamkanize malaya ako. Munthu aliyense akakupempha kanthu, umpatse; ndi iye amene alanda zako, usazipemphanso. Ndipo monga mufuna inu kuti anthu adzakuchitirani inu, muwachitire iwo motero inu momwe. Ndipo ngati muwakonda iwo akukondana ndinu, mudzalandira chiyamiko chotani? Pakuti ochimwa omwe akonda iwo akukondana nao. Ndipo ngati muwachitira zabwino iwo amene akuchitirani inu zabwino, mudzalandira chiyamiko chotani? Pakuti anthu ochimwa omwe amachita chomwecho. Ndipo ngati mukongoletsa kanthu kwa iwo amene muyembekeza kulandiranso, mudzalandira chiyamiko chotani? Pakuti inde anthu ochimwa amakongoletsa kwa ochimwa anzao, kuti alandirenso momwemo. Koma takondanani nao adani anu, ndi kuwachitira zabwino, ndipo kongoletsani osayembekeza kanthu konse, ndipo mphotho yanu idzakhala yaikulu, ndipo inu mudzakhala ana a Wamkulukuluyo; chifukwa Iye achitira zokoma anthu osayamika ndi oipa. Khalani inu achifundo monga Atate wanu ali wachifundo. Ndipo musamaweruza, ndipo simudzaweruzidwa. Ndipo musawatsutsa, ndipo simudzamatsutsidwa. Khululukani, ndipo mudzakhululukidwa. Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokuchumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m'manja mwanu. Pakuti kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nao inu. Ndipo Iye ananenanso nao fanizo, Kodi munthu wakhungu angathe kutsogolera mnzake wakhungu? Kodi sadzagwa onse awiri m'mbuna? Wophunzira saposa mphunzitsi wake; koma yense, m'mene atakonzedwa mtima, adzafanana ndi mphunzitsi wake. Ndipo uyang'aniranji kachitsotso kali m'diso la mbale wako, koma mtanda wa m'diso la iwe mwini suuzindikira? Kapena ungathe bwanji kunena kwa mbale wako, Mbale iwe, leka ndichotse kachitsotso kali m'diso lako, wosayang'anira iwe mwini mtanda uli m'diso lako? Wonyenga iwe! Thanga wachotsa mtandawo m'diso lako, ndipo pomwepo udzayang'anitsa bwino kuchotsa kachitsotso ka m'diso la mbale wako. Pakuti palibe mtengo wabwino wakupatsa zipatso zovunda; kapenanso mtengo woipa wakupatsa zipatso zabwino. Pakuti mtengo uliwonse uzindikirika ndi chipatso chake. Pakuti anthu samatchera nkhuyu paminga, kapena pamtungwi samatchera mphesa. Munthu wabwino atulutsa zabwino m'chuma chokoma cha mtima wake; ndi munthu woipa atulutsa zoipa m'choipa chake: pakuti m'kamwa mwake mungolankhula mwa kuchuluka kwa mtima wake. Ndipo munditchuliranji Ine, Ambuye, Ambuye, ndi kusachita zimene ndizinena? Munthu aliyense wakudza kwa Ine, ndi kumva mau anga, ndi kuwachita, ndidzakusonyezani amene afanana naye. Iye afanafana ndi munthu wakumanga nyumba, amene anakumba pansi ndithu, namanga maziko a nyumbayo pathanthwe; ndipo pamene panadza chigumula, mtsinje unagunda pa nyumbayo, ndipo sunakhoza kuigwedeza; chifukwa idamangika bwino. Koma iye amene akumva, ndi kusachita, afanafana ndi munthu wakumanga nyumba pa nthaka yopanda maziko; pa imeneyo unagunda mtsinje, ndipo inagwa pomwepo; ndipo kugumuka kwake kwa nyumbayo kunali kwakukulu. Pamene Yesu adamaliza mau ake onse m'makutu a anthu, analowa m'Kapernao. Ndipo kapolo wa kenturiyo, wokondedwa naye, anadwala, nafuna kutsirizika. Ndipo pamene iye anamva za Yesu, anatuma kwa Iye akulu a Ayuda, namfunsa Iye kuti adze kupulumutsa kapolo wake. Ndipo iwo, pakufika kwa Yesu, anampempha Iye koumirira, nati, Ayenera iye kuti mumchitire ichi; pakuti akonda mtundu wathu, ndipo anatimangira ife sunagoge. Ndipo Yesu anapita nao. Ndipo pakufika Iye tsono pafupi panyumba yake, kenturiyo anatuma kwa Iye abwenzi ake, kunena naye, Ambuye, musadzivute; pakuti sindiyenera ine kuti mudzalowe pansi pa chindwi langa; chifukwa chake ine sindinadziyesera ndekha woyenera kudza kwa Inu: koma nenani mau, ndipo mnyamata wanga adzachiritsidwa. Pakuti inenso ndili munthu wakumvera akulu anga, ndili nao asilikali akumvera ine: ndipo ndinena kwa uyu, Muka, namuka; ndi kwa wina, Idza, nadza; ndipo kwa kapolo wanga Tachita ichi, nachita. Koma Yesu pakumva zimenezo anazizwa naye, napotolokera kwa anthu a mpingo wakumtsata Iye, nati, Ndinena kwa inu, sindinapeza, ngakhale mwa Israele, chikhulupiriro chachikulu chotere. Ndipo pakubwera kunyumba otumidwawo, anapeza kapoloyo wachira ndithu. Ndipo kunali, katapita kamphindi, Iye anapita kumudzi, dzina lake Naini; ndipo ophunzira ake ndi mpingo waukulu wa anthu anapita naye. Ndipo pamene anayandikira kuchipata cha mudziwo, onani, anthu analikunyamula munthu wakufa, mwana wamwamuna mmodzi yekha, amake ndiye mkazi wamasiye; ndipo anthu ambiri akumudzi anali pamodzi naye. Ndipo pamene Ambuye anamuona, anagwidwa ndi chifundo chifukwa cha iye, nanena naye, Usalire. Ndipo anayandikira, nakhudza chithatha; ndipo akumnyamulawo anaima. Ndipo Iye anati, Mnyamata iwe, ndinena ndi iwe, Tauka. Ndipo wakufayo anakhala tsonga, nayamba kulankhula. Ndipo anampereka kwa amake. Ndipo mantha anagwira onsewo: ndipo analemekeza Mulungu, nanena kuti, Mneneri wamkulu wauka mwa ife; ndipo Mulungu wadzacheza ndi anthu ake. Ndipo mbiri yake imeneyo inabuka ku Yudeya lonse, ndi ku dziko lonse loyandikira. Ndipo ophunzira a Yohane anamuuza iye zonsezi. Ndipo Yohane anaitana awiri a ophunzira ake, nawatuma kwa Ambuye, nanena, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang'anire wina? Ndipo pakufika kwa Iye anthu awo, anati, Yohane Mbatizi watituma ife kwa Inu, kuti, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang'anire wina? Nthawi yomweyo Iye anachiritsa anthu ambiri nthenda zao, ndi zovuta, ndi ziwanda; napenyetsanso anthu akhungu ambiri. Ndipo anayankha, nati kwa iwo, Mukani, muuze Yohane zimene mwaziona, nimwazimva; anthu akhungu alandira kuona kwao, opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ogontha akumva, akufa aukitsidwa, kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino. Ndipo wodala iye amene sakhumudwa chifukwa cha Ine. Ndipo atachoka amithenga ake a Yohane, Iye anayamba kunena za Yohane kwa anthu a makamu aja, nati, Munatuluka kunka kuchipululu kukapenya chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi? Koma munatuluka kukaona chiyani? Munthu wovala zovala zofewa kodi? Onani, iwo akuvala zolemera, ndi akukhala odyerera, ali m'nyumba za mafumu. Koma munatuluka kukaona chiyani? Mneneri kodi? Etu, ndinena kwa inu, ndipo wakuposa mneneri. Uyu ndi iye amene kunalembedwa za iye, Ona, ndituma Ine mthenga wanga akutsogolere, amene adzakukonzera njira yako pamaso pako. Ndinena kwa inu, kuti, Mwa akubadwa ndi akazi palibe mmodzi wamkulu woposa Yohane; koma iye amene ali wamng'ono mu Ufumu wa Mulungu amposa iye. Ndipo anthu onse ndi amisonkho omwe, pakumva, anavomereza kuti Mulungu ali wolungama, popeza anabatizidwa iwo ndi ubatizo wa Yohane. Koma Afarisi ndi achilamulo anakaniza uphungu wa Mulungu kwa iwo okha, popeza sanabatizidwe ndi iye. Ndipo, ndidzafanizira ndi chiyani anthu a mbadwo uno? Ndipo afanana ndi chiyani? Angofanana ndi ana akukhala pamsika, ndi kuitanizana wina ndi mnzake, ndi kunena, Ife tinakulizirani chitoliro, ndipo inu simunavina ai; tinabuma maliro, ndimo simunalira ai. Pakuti Yohane Mbatizi wafika wosadya mkate ndi wosamwa vinyo; ndipo munena, Ali ndi chiwanda. Mwana wa Munthu wafika wakudya ndi wakumwa; ndipo munena, Onani, munthu wosusuka ndi wakumwaimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi anthu ochimwa! Ndipo nzeru iyesedwa yolungama ndi ana ake onse. Ndipo mmodzi wa Afarisi anamuitana Iye kuti akadye naye. Ndipo analowa m'nyumba ya Mfarisi, naseama pachakudya. Ndipo onani, mkazi wochimwa, amene anali m'mudzimo; ndipo pakudziwa kuti Yesu analikuseama pachakudya m'nyumba ya Mfarisi, anatenga nsupa ya alabastero ya mafuta onunkhira bwino, naimirira kumbuyo, pa mapazi ake, nalira, nayamba kukhathamiza mapazi ake ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi la mutu wake, nampsompsonetsa mapazi ake, nawadzoza ndi mafuta onunkhira bwino. Koma Mfarisi, amene adamuitana Iye, pakuona, ananena mwa yekha, nati, Akadakhala mneneri uyu akadazindikira ali yani, ndi wotani mkaziyo womkhudza Iye, chifukwa ali wochimwa. Ndipo Yesu anayankha nati kwa iye, Simoni, ndili ndi kanthu kakunena kwa iwe. Ndipo iye anavomera, Mphunzitsi, nenani. Munthu wokongoletsa ndalama anali nao amangawa awiri; mmodziyo anali ndi mangawa ake a marupiya mazana asanu, koma mnzake makumi asanu. Popeza analibe chobwezera iwo, anawakhululukira onse awiri. Chotero, ndani wa iwo adzaposa kumkonda? Simoni anayankha, nati, Ndiyesa kuti, iye amene anamkhululukira zoposa. Ndipo anati kwa iye, Waweruza bwino. Ndipo m'mene Iye anacheukira kwa mkaziyo, anati kwa Simoni, Upenya mkazi ameneyu kodi? Ndinalowa m'nyumba yako, sunandipatsa madzi akusambitsa mapazi anga; koma uyu anakonkha mapazi anga ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi lake. Sunandipatsa mpsompsono wa chibwenzi; koma uyu sanaleke kupsompsonetsa mapazi anga, chilowere muno Ine. Sunandidzoza mutu wanga ndi mafuta; koma uyu anadzoza mapazi anga ndi mafuta onunkhira bwino. Chifukwa chake, ndinena kwa iwe, Machimo ake, ndiwo ambiri, akhululukidwa; chifukwa anakonda kwambiri; koma munthu amene anamkhululukira pang'ono, iye akonda pang'ono. Ndipo anati kwa mkazi, Machimo ako akhululukidwa. Ndipo iwo akuseama naye pachakudya anayamba kunena mwa okha, Uyu ndani amene akhululukiranso machimo? Ndipo Iye anati kwa mkaziyo, Chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe; muka ndi mtendere. Ndipo kunali, katapita kamphindi anayendayenda kumizinda ndi kumidzi, kulalikira ndi kuwauza Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndi pamodzi naye khumi ndi awiriwo, ndi akazi ena amene anachiritsidwa ziwanda ndi nthenda zao, ndiwo, Maria wonenedwa Magadala, amene ziwanda zisanu ndi ziwiri zinatuluka mwa iye, ndi Yohana, mkazi wake wa Kuza kapitao wa Herode, ndi Suzana, ndi ena ambiri, amene anawatumikira ndi chuma chao. Ndipo pamene khamu lalikulu la anthu linasonkhana, ndi anthu a kumidzi yonse anafika kwa Iye, anati mwa fanizo: Anatuluka wofesa kukafesa mbeu zake; ndipo m'kufesa kwake zina zinagwa m'mbali mwa njira; ndipo zinapondedwa, ndi mbalame za m'mlengalenga zinatha kuzidya. Ndipo zina zinagwa pathanthwe; ndipo pakumera zinatofa msanga, chifukwa zinalibe mnyontho. Ndipo zina zinagwa pakati pa minga; ndi mingayo inaphuka pamodzi nazo, nizitsamwitsa. Ndipo zina zinagwa pa nthaka yokoma, ndipo zinamera, ndi kupatsa zipatso zamakumikhumi. Pakunena Iye izi anafuula, Iye amene ali ndi makutu akumva amve. Ndipo ophunzira ake anamfunsa Iye, kuti, Fanizo ili lili lotani? Ndipo Iye anati, Kwapatsidwa kwa inu kuzindikira zinsinsi za Ufumu wa Mulungu; koma kwa ena otsala ndinena nao mwa mafanizo; kuti pakuona sangaone, ndi pakumva sangadziwitse. Koma fanizoli litere: Mbeuzo ndizo mau a Mulungu. Ndipo za m'mbali mwa njira ndiwo anthu amene adamva; pamenepo akudza mdierekezi, nachotsa mau m'mitima yao, kuti angakhulupirire ndi kupulumuka. Ndipo za pathanthwe ndiwo amene, pakumva, alandira mau ndi kukondwera; koma alibe mizu; akhulupirira kanthawi, ndipo pa nthawi ya mayesedwe angopatuka. Ndipo zija zinagwa kumingazi, ndiwo amene adamva, ndipo m'kupita kwao atsamwitsidwa ndi nkhawa, ndi chuma, ndi zokondweretsa za moyo, ndipo sakhwimitsa zipatso zamphumphu. Ndipo zija za m'nthaka yokoma, ndiwo amene anamva mau nawasunga mu mtima woona ndi wabwino, nabala zipatso ndi kupirira. Ndipo palibe munthu atayatsa nyali, aivundikira ndi chotengera, kapena kuiika pansi pa kama; koma aiika pa choikapo, kuti iwo akulowamo aone kuunikaku. Pakuti palibe chinthu chobisika, chimene sichidzakhala choonekera; kapena chinsinsi chimene sichidzadziwika ndi kuvumbuluka. Chifukwa chake yang'anirani mamvedwe anu; pakuti kudzapatsidwa kwa iye amene ali nacho; ndipo kwa iye amene alibe chidzachotsedwa, chingakhale chija aoneka ngati ali nacho. Ndipo anadza kwa Iye amake ndi abale ake, ndipo sanakhoze kumfika, chifukwa cha khamu la anthu. Ndipo anamuuza Iye, kuti, Amai wanu ndi abale anu alinkuima kunja, nafuna kuona Inu. Koma Iye anayankha, nati kwa iwo, Amai wanga ndi abale anga ndiwo amene akumva mau a Mulungu, nawachita. Ndipo panali limodzi la masiku aja, Iye analowa m'ngalawa, ndi ophunzira ake; nati kwa iwo, Tiolokere kutsidya lija la nyanja; ndipo anakankhiramo. Ndipo m'mene iwo anali kupita pamadzi, Iye anagona tulo. Ndipo panyanja panatsikira namondwe wa mphepo; ndipo podzala ndi madzi, analimkuopsedwa. Ndipo anadza kwa Iye, namuutsa, nanena, Ambuye, Ambuye, titayika. Ndipo anauka, nadzudzula mphepo ndi mafunde ake a madzi; pomwepo zinaleka, ndipo panagwa bata. Ndipo Iye anati kwa iwo, Chikhulupiriro chanu chili kuti? Ndipo m'kuchita mantha anazizwa iwo, nanena wina ndi mnzake, Uyu ndani nanga, kuti angolamula mphepo ndi madzi, ndipo zimvera Iye? Ndipo iwo anakocheza kudooko ku dziko la Agerasa, ndilo lopenyana ndi Galileya. Ndipo atatuluka pamtunda Iye, anakomana naye mwamuna wa kumudzi, amene anali nazo ziwanda; ndipo masiku ambiri sanavale chovala, nisanakhala m'nyumba, koma m'manda. Ndipo pakuona Yesu, iye anafuula, nagwa pansi pamaso pake, nati ndi mau akulu, Ndili nacho chiyani ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkulukulu? Ndikupemphani Inu musandizunze. Pakuti Iye adalamula mzimu wonyansa utuluke mwa munthuyo. Pakuti nthawi zambiri unamgwira; ndipo anthu anammanga ndi maunyolo ndi matangadza kumsungira; ndipo anamwetula zomangirazo, nathawitsidwa ndi chiwandacho kumapululu. Ndipo Yesu anamfunsa iye, kuti, Dzina lako ndiwe yani? Ndipo anati, Legio, chifukwa ziwanda zambiri zidalowa mwa iye. Ndipo zinampempha Iye, kuti asazilamulire zichoke kulowa ku chiphompho chakuya. Ndipo panali pamenepo gulu la nkhumba zambiri zilinkudya m'phiri. Ndipo zinampempha Iye kuti azilole zilowe mu izo. Ndipo anazilola. Ndipo ziwandazo zinatuluka mwa munthu nizilowa mu nkhumba: ndipo gululo linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m'nyanjamo, nilitsamwa. Ndipo akuwetawo m'mene anaona chimene chinachitika, anathawa, nauza akumudzi ndi kumilaga yake. Ndipo iwo anatuluka kukaona chimene chinachitika; ndipo anadza kwa Yesu, nampeza munthuyo, amene ziwanda zinatuluka mwa iye, alikukhala pansi kumapazi ake a Yesu wovala ndi wa nzeru zake; ndipo iwo anaopa. Ndipo amene anaona anawauza iwo machiritsidwe ake a wogwidwa chiwandayo. Ndipo anthu aunyinji onse a dziko la Agerasa loyandikira anamfunsa Iye achoke kwa iwo; chifukwa anagwidwa ndi mantha akulu. Ndipo Iye analowa m'ngalawa, nabwerera. Ndipo munthuyo amene ziwanda zinatuluka mwa iye anampempha Iye akhale ndi Iye; koma anamuuza apite, nanena, Pita kunyumba kwako, nufotokozere zazikuluzo anakuchitira iwe Mulungu. Ndipo iye anachoka, nalalikira kumudzi wonse zazikuluzo Yesu anamchitira iye. Ndipo pakubwera Yesu, khamu la anthu linamlandira Iye; pakuti onse analikumlindira Iye. Ndipo onani, panadza munthu dzina lake Yairo, ndipo iye ndiye mkulu wa sunagoge; ndipo anagwa pamapazi ake a Yesu, nampempha Iye adze kunyumba kwake; chifukwa anali naye mwana wamkazi mmodzi yekha, wa zaka zake ngati khumi ndi ziwiri, ndipo analinkumwalira iye. Koma pakupita Iye anthu a mipingo anakanikizana naye. Ndipo mkazi, anali ndi nthenda yachidwalire zaka khumi ndi ziwiri, amene adasudzula asing'anga za moyo wake zonse, ndipo sanathe kuchiritsidwa ndi mmodzi yense, anadza pambuyo pake, nakhudza mphonje ya chovala chake; ndipo pomwepo nthenda yake inaleka. Ndipo Yesu anati, Wandikhudza Ine ndani? Koma pamene onse anakana, Petro ndi iwo akukhala naye anati, Ambuye, anthu aunyinji alikukankhana pa Inu ndi kukanikizana. Koma Yesu anati, Wina wandikhudza Ine; pakuti ndazindikira Ine kuti mphamvu yatuluka mwa Ine. Ndipo mkaziyo pakuona kuti sanabisike, anadza ndi kunthunthumira, nagwa pamaso pake, nafotokoza pamaso pa anthu onsewo chifukwa chake cha kumkhudza Iye, ndi kuti anachiritsidwa pomwepo. Ndipo Iye anati kwa iyeyu, Mwana wanga, chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe; muka ndi mtendere. M'mene Iye anali chilankhulire, anadza wina wochokera kwa mkulu wa sunagoge, nanena, Mwana wako wafa; usamvute Mphunzitsi. Koma Yesu anamva, namyankha, kuti, Usaope; khulupirira kokha, ndipo iye adzapulumutsidwa. Ndipo pakufika Iye kunyumbako, sanaloleze wina kulowa naye pamodzi, koma Petro, ndi Yohane, ndi Yakobo, ndi atate wa mwanayo, ndi amake. Ndipo anthu onse analikumlirira iye ndi kudziguguda pachifuwa. Koma Iye anati, Musalire; pakuti iye sanafe, koma wagona tulo. Ndipo anamseka Iye pwepwete podziwa kuti anafa. Ndipo Iye anamgwira dzanja lake, naitana, nati, Buthu, tauka. Ndipo mzimu wake unabwera, ndipo anauka pomwepo; ndipo Iye anawauza kuti ampatse kanthu ka kudya. Ndipo atate wake ndi amake anadabwa; ndipo analamulira iwo asauze munthu aliyense chimene chinachitika. Ndipo Iye anaitana pamodzi khumi ndi awiriwo nawapatsa mphamvu ndi ulamuliro pa ziwanda zonse, ndi zakuchiritsa nthenda. Ndipo anawatuma kukalalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuchiritsa anthu odwala. Ndipo Iye anati kwa iwo, Musanyamule kanthu ka paulendo, kapena ndodo, kapena thumba, kapena mkate, kapena ndalama; ndipo musakhale nao malaya awiri. Ndipo m'nyumba iliyonse mukalowemo, khalani komweko, ndipo muzikachokera kumeneko. Ndipo onse amene sakakulandireni inu, m'mene mutuluka m'mudzi womwewo, sansani fumbi la pa mapazi anu, likhale mboni ya paiwo. Ndipo iwo anatuluka, napita m'midzi yonse, ndi kulalikira Uthenga Wabwino, ndi kuchiritsa ponse. Ndipo Herode chiwangacho anamva mbiri yake ya zonse zinachitika; ndipo inamthetsa nzeru, chifukwa ananena anthu ena, kuti Yohane anauka kwa akufa; koma ena, kuti Eliya anaoneka; ndipo ena, kuti mneneri wina wa akale aja anauka. Ndipo Herode anati, Yohane ndinamdula mutu ine; koma uyu ndani ndikumva zotere za iye? Ndipo anafunafuna kumuona Iye. Ndipo atabwera atumwi, anamfotokozera Iye zonse anazichita. Ndipo Iye anawatenga, napatuka nao pa okha kunka kumudzi dzina lake Betsaida. Koma unyinji wa anthu, pamene anadziwa, anamtsata Iye; ndipo Iye anawalandira, nalankhula nao za Ufumu wa Mulungu, nachiritsa amene anasowa kuchiritsidwa. Koma dzuwa lidapendeka; ndipo khumi ndi awiriwo anadza, nati kwa Iye, Tauzani makamu a anthu amuke, kuti apite kumidzi yoyandikira ndi kumilaga, kukafuna pogona, ndi kupeza zakudya; chifukwa tili kumalo achipululu kuno. Koma anati kwa iwo, Muwapatse kudya ndinu. Koma anati, Ife tilibe mikate, koma isanu yokha, ndi nsomba ziwiri zokha; kapena timuke ife kukagulira anthu awa onse zakudya. Pakuti anali amuna ngati zikwi zisanu. Koma Iye anati kwa ophunzira ake, Khalitsani iwo pansi magulumagulu, ngati makumi asanuasanu. Ndipo anatero, nawakhalitsa pansi onsewo. Ndipo Iye, m'mene anatenga mikate isanu ija ndi nsomba ziwiri anayang'ana kumwamba, nazidalitsa, nanyema, napatsa ophunzira apereke kwa anthuwo. Ndipo anadya, nakhuta onsewo; natola makombo, madengu khumi ndi awiri. Ndipo kunali, pamene Iye anali kupemphera padera, ophunzira anali naye; ndipo anawafunsa iwo, kuti, Makamuwo a anthu anena kuti Ine ndine yani? Ndipo anayankha nati, Yohane Mbatizi; koma ena, Eliya; ndi ena, kuti anauka mmodzi wa aneneri akale. Ndipo anati kwa iwo, Koma inu munena kuti Ine ndine yani? Ndipo anayankha Petro, nati, Khristu wa Mulungu. Ndipo Iye anawauzitsa iwo, nalamulira kuti asanene ichi kwa munthu aliyense; nati, Kuyenera kuti Mwana wa Munthu amve zowawa zambiri, ndi kukanidwa ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi, ndi kuphedwa, ndi kuuka tsiku lachitatu. Ndipo Iye ananena kwa onse, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule mtanda wake tsiku ndi tsiku, nanditsate Ine. Pakuti amene aliyense akafuna kupulumutsa moyo wake, iye adzautaya; koma amene aliyense akataya moyo wake chifukwa cha Ine, iye adzaupulumutsa uwu. Pakuti munthu apindulanji, akadzilemezera dziko lonse lapansi nadzitayapo, kapena kulipapo moyo wake? Pakuti amene aliyense adzachita manyazi chifukwa cha Ine ndi mau anga, Mwana wa Munthu adzachita manyazi chifukwa cha iye, pamene adzafika ndi ulemerero wake ndi wa Atate, ndi wa angelo oyera. Koma Ine ndinena ndi inu zoonadi, Kuli ena a iwo akuimirira pano, amene sadzalawatu imfa, kufikira kuti adzaona Ufumu wa Mulungu. Ndipo pamene padatha ngati masiku asanu ndi atatu atanena mau amenewa, Iye anatenga Petro ndi Yohane ndi Yakobo apite naye, nakwera m'phiri kukapemphera. Ndipo m'kupemphera kwake, maonekedwe a nkhope yake anasandulika, ndi chovala chake chinayera ndi kunyezimira. Ndipo onani, analikulankhulana naye amuna awiri, ndiwo Mose ndi Eliya; amene anaonekera m'ulemerero, nanena za kumuka kwake kumene Iye ati adzatsiriza ku Yerusalemu. Koma Petro ndi iwo anali naye analemedwa ndi tulo; koma m'mene anayera m'maso ndithu, anaona ulemerero wake, ndi amuna awiriwo akuimirira ndi Iye. Ndipo panali polekana iwo aja ndi Iye, Petro anati kwa Yesu, Ambuye, nkwabwino kuti tili pano; ndipo timange misasa itatu, umodzi wa Inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya; wosadziwa iye chimene alikunena. Ndipo akadalankhula izi, unadza mtambo, nuwaphimba iwo; ndipo anaopa pakulowa iwo mumtambo. Ndipo munatuluka mau mumtambo, nanena, Uyu ndiye Mwana wanga, wosankhidwayo; mverani Iye. Ndipo pakutero mauwo, Yesu anapezedwa ali yekha. Ndipo iwo anakhala chete, ndipo sanauze munthu aliyense masiku aja kanthu konse ka izo anaziona. Ndipo panali, m'mawa mwake, atatsika m'phiri, khamu lalikulu la anthu linakomana naye. Ndipo onani, anafuula munthu wa m'khamulo, nanena, nati, Mphunzitsi, ndikupemphani, yang'anirani mwana wanga; chifukwa ndiye mmodzi yekha wa ine: ndipo onani, umamgwira iye mzimu, nafuula modzidzimuka; ndipo umamng'amba iye ndi kumchititsa thovu pakamwa, nuchoka pa iye mwa unyenzi, numgola iye. Ndipo ndinapempha ophunzira anu kuti autulutse; koma sanathe. Ndipo Yesu anayankha, nati, Ha! Obadwa inu osakhulupirira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji, ndi kulekerera inu? Idza naye kuno mwana wako. Ndipo akadadza iye, chiwandacho chinamgwetsa, ndi kumng'ambitsa. Koma Yesu anadzudzula mzimu wonyansawo, nachiritsa mnyamata, nambwezera iye kwa atate wake. Ndipo onse anadabwa pa ukulu wake wa Mulungu. Koma pamene onse analikuzizwa ndi zonse anazichita, Iye anati kwa ophunzira ake, Alowe mau amenewa m'makutu anu; pakuti Mwana wa Munthu adzaperekedwa m'manja a anthu. Koma iwo sanadziwitse mau awa, ndipo anabisidwa kwa iwo, kuti asawadziwe; ndipo anaopa kumfunsa za mau awa. Ndipo anayamba kutsutsana kuti wamkulu mwa iwo ndani. Koma Yesu pakuona kutsutsana kwa mitima yao, anatenga kamwana, nakaimika pambali pake, nati kwa iwo, Amene aliyense akalandire kamwana aka m'dzina langa alandira Ine; ndipo amene andilandira Ine alandira Iye amene anandituma Ine; pakuti iye wakukhala wamng'onong'ono wa inu nonse, yemweyu ndiye wamkulu. Ndipo Yohane anayankha nati, Ambuye, tinaona wina alikutulutsa ziwanda m'dzina lanu; ndipo tinamletsa, chifukwa satsatana nafe. Koma Yesu anati kwa iye, Musamletse, pakuti iye amene satsutsana nanu athandizana nanu. Ndipo panali, pamene anayamba kukwanira masiku akuti alandiridwe Iye kumwamba, Yesu anatsimikiza kuloza nkhope yake kunka ku Yerusalemu, natumiza amithenga patsogolo pake; ndipo ananka, nalowa m'mudzi wa Asamariya, kukamkonzera Iye malo. Ndipo iwo sanamlandire Iye, chifukwa nkhope yake inali yoloza kunka ku Yerusalemu. Ndipo pamene ophunzira ake Yakobo ndi Yohane anaona, anati, Ambuye, Kodi mufuna kuti ife tiuze moto utsike kumwamba ndi kuwanyeketsa iwo? Koma Iye anapotoloka nawadzudzula. Ndipo anapita kumudzi kwina. Ndipo m'mene iwo analikuyenda m'njira, munthu anati kwa Iye, Ine ndidzakutsatani kumene kulikonse mukapitako. Ndipo Yesu anati kwa iye, Nkhandwe zili nazo nkhwimba, ndi mbalame za kumwamba zisa, koma Mwana wa Munthu alibe potsamira mutu. Ndipo anati kwa munthu wina, Unditsate Ine. Koma iye anati, Mundilole ine, Ambuye, ndithange ndamuka kuika maliro a atate wanga. Koma anati kwa iye, Leka akufa aike akufa a eni okha; koma muka iwe nubukitse mbiri yake ya Ufumu wa Mulungu. Ndipo winanso anati, Ambuye ndidzakutsatani Inu; koma muthange mwandilola kulawirana nao a kunyumba kwanga. Koma Yesu anati kwa iye, Palibe munthu wakugwira chikhasu, nayang'ana za kumbuyo, ayenera Ufumu wa Mulungu. Zitapita izi Ambuye anaika ena makumi asanu ndi awiri, nawatuma iwo awiriawiri pamaso pake kumudzi uliwonse, ndi malo ali onse kumene ati afikeko mwini. Ndipo ananena kwa iwo, Dzinthu dzichuluka, koma antchito achepa; potero pemphani Mwini dzinthu, kuti akankhe antchito kukututa kwake. Mukani; taonani, Ine ndituma inu ngati anaankhosa pakati pa mimbulu. Musanyamule thumba la ndalama kapena thumba la kamba, kapena nsapato; nimusalonjere munthu panjira. Ndipo m'nyumba iliyonse mukalowamo muthange mwanena, Mtendere ukhale pa nyumba iyi. Ndipo mukakhala mwana wa mtendere m'menemo, mtendere wanu udzapumula pa iye; koma ngati mulibe, udzabwerera kwa inu. Ndipo m'nyumba momwemo khalani, ndi kudya ndi kumwa za kwao; pakuti wantchito ayenera mphotho yake; musachokachoka m'nyumba. Ndipo m'mudzi uliwonse mukalowamo, ndipo alandira inu, idyani zomwezi akupatsani; ndipo chiritsani odwala ali momwemo nimunene nao, Ufumu wa Mulungu wayandikira kwa inu. Koma kumudzi uliwonse mukalowako, ndipo salandira inu, m'mene mwatuluka kumakwalala ake nenani, Lingakhale fumbi lochokera kumudzi kwanu, lomamatika kumapazi athu, tilisansira pa inu; koma zindikirani ichi, kuti Ufumu wa Mulungu wayandikira. Ndinena ndi inu kuti tsiku lijalo ku Sodomu kudzapiririka kuposa mudzi umenewo. Tsoka iwe, Korazini! Tsoka iwe Betsaida! Chifukwa kuti zikadachitika m'Tiro ndi Sidoni zamphamvuzi zidachitika mwa inu, akadalapa kale lomwe ndi kukhala pansi ovala chiguduli ndi phulusa. Koma ku Tiro ndi Sidoni kudzapiririka m'chiweruziro, koposa inu. Ndipo iwe, Kapernao, kodi udzakwezedwa kufikira Kumwamba? Udzatsitsidwa kufikira ku dziko la akufa. Iye wakumvera inu, andimvera Ine; ndipo iye wakukana inu, andikana Ine; ndipo iye wakukana Ine amkana Iye amene anandituma Ine. Ndipo makumi asanu ndi awiri aja anabwera mokondwera, nanena, Ambuye, zingakhale ziwanda zinatigonjera ife m'dzina lanu. Ndipo anati kwa iwo, Ndinaona Satana alinkugwa ngati mphezi wochokera kumwamba. Taonani, ndakupatsani ulamuliro wakuponda pa njoka ndi zinkhanira, ndi pa mphamvu iliyonse ya mdaniyo; ndipo kulibe kanthu kadzakuipsani konse. Koma musakondwera nako kuti mizimu idakugonjerani, koma kondwerani kuti maina anu alembedwa m'Mwamba. Nthawi yomweyo Iye anakondwera ndi Mzimu Woyera, nati, Ndikuvomerezani Inu, Atate, Ambuye wa kumwamba ndi wa dziko, kuti izi munazibisira anzeru ndi ozindikira, ndipo munaziululira ana amakanda; indedi, Atate, pakuti kotero kudakondweretsa pamaso panu. Zonse zaperekedwa kwa Ine ndi Atate wanga; ndipo palibe munthu azindikira Mwana ali yani, koma Atate; ndipo Atate ali yani, koma Mwana, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira Iye. Ndipo m'mene anapotolokera kwa ophunzira ake, ali pa okha, anati, Odala masowo akuona zimene muona. Pakuti ndinena ndi inu kuti aneneri ndi mafumu ambiri anafuna kuona zimene inu muziona, koma sanazione; ndi kumva zimene mukumva, koma sanazimve. Ndipo taonani, wachilamulo wina anaimirira namuyesa Iye, nanena, Mphunzitsi, ndidzalowa moyo wosatha ndi kuchita chiyani? Ndipo anati kwa iye, M'chilamulo mulembedwa chiyani? Uwerenga bwanji? Ndipo iye anayankha nati, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu yako yonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mnansi wako monga iwe mwini. Ndipo anati kwa iye, Wayankha bwino; chita ichi, ndipo udzakhala ndi moyo. Koma iye, pofuna kudziyesa yekha wolungama, anati kwa Yesu, Ndipo mnansi wanga ndani? Ndipo Yesu anamlanda mau, nati, Munthu wina anatsika kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Yeriko; ndipo anagwa m'manja a achifwamba amene anamvula zovala, namkwapula, nachoka atamsiya wofuna kufa. Ndipo kudangotero kuti wansembe wina anatsika njirayo, ndipo pakumuona iye anapita mbali ina. Momwemonso Mlevi, pofika pamenepo, ndi kumuona, anapita mbali ina. Koma Msamariya wina ali pa ulendo wake anadza pali iye; ndipo pakumuona, anagwidwa chifundo, nadza kwa iye, namanga mabala ake, nathirapo mafuta ndi vinyo; ndipo anamuika iye pa nyama yake ya iye yekha, nadza naye kunyumba ya alendo, namsungira. Ndipo m'mawa mwake anatulutsa marupiya atheka awiri napatsa mwini nyumba ya alendo, nati, Msungire iye, ndipo chilichonse umpatsa koposa, ine, pobwera, ndidzakubwezera iwe. Uti wa awa atatu, uyesa iwe, anakhala mnansi wa iye uja adagwa m'manja a achifwamba? Ndipo anati, Iye wakumchitira chifundo. Ndipo Yesu anati kwa iye, Pita nuchite iwe momwemo. Ndipo pakupita paulendo pao Iye analowa m'mudzi wina; ndipo mkazi wina dzina lake Marita anamlandira Iye kunyumba kwake. Ndipo anali ndi mbale wake wotchedwa Maria, ndiye wakukhala pa mapazi a Ambuye, namva mau ake. Koma Marita anatekeseka ndi kutumikira kwambiri; ndipo anadzako nati, Ambuye, kodi simusamala kuti mbale wanga anandisiya nditumikire ndekha? Mumuuze tsono kuti andithandize. Koma Ambuye anayankha nati kwa iye, Marita, Marita, uda nkhawa nuvutika ndi zinthu zambiri; koma chisoweka chinthu chimodzi, pakuti Maria anasankha dera lokoma limene silidzachotsedwa kwa iye. Ndipo kunali, pakukhala Iye pamalo pena ndi kupemphera, m'mene analeka, wina wa ophunzira ake anati kwa Iye, Ambuye, tiphunzitseni ife kupemphera, monganso Yohane anaphunzitsa ophunzira ake. Ndipo anati kwa iwo, M'mene mupemphera nenani, Atate, Dzina lanu liyeretsedwa; Ufumu wanu udze; tipatseni ife tsiku ndi tsiku chakudya cha patsiku. Ndipo mutikhululukire ife machimo athu; pakuti ifenso tikhululukira munthu yense wa mangawa athu. Ndipo musatitengere ife kokatiyesa. Ndipo anati kwa iwo, Ndani wa inu adzakhala ndi bwenzi lake, nadzapita kwa iye pakati pa usiku, nadzati kwa iye, Bwenzi, ndibwereke mikate itatu; popeza wandidzera ndipo ndilibe chompatsa; ndipo iyeyu wa m'katimo poyankha akati, Usandivuta; pakhomo mpotseka tsopano, ndipo ana anga ali nane pamodzi pogona; sindikhoza kuuka ndi kukupatsa? Ndinena ndi inu, ngakhale sadzauka ndi kumpatsa, chifukwa ali bwenzi lake, koma chifukwa cha liuma lake adzauka nadzampatsa iye zilizonse azisowa. Ndipo Ine ndinena ndi inu, Pemphani, ndipo adzakupatsani; funani, ndipo mudzapeza; gogodani ndipo adzakutsegulirani. Pakuti yense wakupempha alandira; ndi wofuna apeza; ndi iye amene agogoda adzamtsegulira. Ndipo ndani wa inu ali atate, mwana wake akadzampempha mkate, adzampatsa mwala? Kapena nsomba, nadzamninkha njoka m'malo mwa nsomba? Kapena akadzampempha dzira kodi adzampatsa chinkhanira? Potero, ngati inu, okhala oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha Iye? Ndipo analikutulutsa chiwanda chosalankhula. Ndipo kunali, chitatuluka chiwanda, wosalankhulayo analankhula; ndipo makamu a anthu anazizwa. Koma ena mwa iwo anati, Ndi Belezebulu mkulu wa ziwanda amatulutsa ziwanda. Koma ena anamuyesa, nafuna kwa Iye chizindikiro chochokera Kumwamba. Koma Iye, podziwa zolingirira zao, anati kwa iwo, Ufumu uliwonse wogawanika m'kati mwake upasuka; ndipo nyumba ikagawanika m'kati mwake igwa. Ndiponso ngati Satana agawanika kudzitsutsa mwini, udzaimika bwanji ufumu wake? Popeza munena kuti nditulutsa ziwanda ndi Belezebulu. Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi Belezebulu, ana anu azitulutsa ndi yani? Mwa ichi iwo adzakhala oweruza anu. Koma ngati Ine nditulutsa ziwanda ndi chala cha Mulungu, pamenepo Ufumu wa Mulungu wafikira inu. Pamene paliponse mwini mphamvu alonda pabwalo pake zinthu zake zili mumtendere; koma pamene paliponse amdzera wakumposa mphamvu, nakamlaka, amchotsera zida zake zonse zimene anazitama, nagawa zofunkha zake. Iye wosavomerezana ndi Ine atsutsana ndi Ine; ndipo iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwaza. Pamene paliponse mzimu wonyansa ukatuluka mwa munthu, upyola malo opanda madzi nufunafuna mpumulo; ndipo posaupeza unena, Ndidzabwera kunyumba kwanga kumene ndinatulukako; ndipo pofika, uipeza yosesa ndi yokonzeka. Pomwepo upita nutenga mizimu ina isanu ndi iwiri yoipa yoposa ndi uwu mwini; ndipo ilowa nikhalira komweko; ndipo makhalidwe otsiriza a munthu uyu aipa koposa oyambawo. Ndipo kunali, pakunena izi Iye, mkazi wina mwa khamu la anthu anakweza mau, nati kwa Iye, Yodala mimba imene idakubalani, ndi mawere amene munayamwa. Koma Iye anati, Inde, koma odala iwo akumva mau a Mulungu, nawasunga. Ndipo pakusonkhana pamodzi makamu a anthu, anayamba kunena, Mbadwo uno ndi mbadwo woipa; ufuna chizindikiro, ndipo chizindikiro sichidzapatsidwa kwa uwu koma chizindikiro cha Yona. Pakuti monga ngati Yona anali chizindikiro kwa Aninive, chotero adzakhalanso Mwana wa Munthu kwa mbadwo uno. Mfumu yaikazi ya kumwera idzaimirira pa mlandu wotsiriza pamodzi ndi amuna a mbadwo uno, nadzawatsutsa; pakuti anadza kuchokera kumalekezero a dziko kudzamva nzeru za Solomoni; ndipo onani, woposa Solomoni ali pano. Amuna a ku Ninive adzaimirira pa mlandu wotsiriza pamodzi ndi anthu a mbadwo uno, nadzawatsutsa; pakuti iwo analapa pa kulalikira kwa Yona; ndipo onani, wakuposa Yona ali pano. Palibe munthu, atayatsa nyali, aiika m'chipinda chapansi, kapena pansi pa mbiya, koma pa choikapo chake, kuti iwo akulowamo aone kuunika. Nyali ya thupi ndiyo diso lako; pamene paliponse diso lako lili langwiro thupi lako lonse liunikidwanso monsemo; koma likakhala loipa, thupi lako lomwe lili la mdima wokhawokha. Potero yang'anira kuunika kuli mwa iwe kungakhale mdima. Pamenepo, ngati thupi lako lonse liunikidwa losakhala nalo dera lake lamdima, lidzakhala lounikidwa monsemo, ngati pamene nyali ndi kuwala kwake ikuunikira iwe. Ndipo pakulankhula Iye, anamuitana Mfarisi kuti adye naye; ndipo analowa naseama kudya. Ndipo anazizwa Mfarisiyo, pakuona kuti anayamba chakudya asanasambe. Koma Ambuye anati kwa iye, Tsopano inu Afarisi muyeretsa kunja kwake kwa chikho ndi mbale, koma m'kati mwanu mudzala zolanda ndi zoipa. Opusa inu, kodi Iye wopanga kunja kwake sanapangenso m'kati mwake? Koma patsani mphatso yachifundo za m'katimo; ndipo onani, zonse zili zoyera kwa inu. Koma tsoka inu, Afarisi! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi timbeu tokometsa chakudya ndi ndiwo zonse, ndipo mumaleka chiweruzo ndi chikondi cha Mulungu; mwenzi mutachita izi, ndi kusasiya zinazo. Tsoka inu, Afarisi! Chifukwa mukonda mipando yaulemu m'masunagoge, ndi kupatsidwa moni m'misika. Tsoka inu! Chifukwa muli ngati manda osaoneka, ndipo anthu akuyendayenda pamwamba pao sadziwa. Ndipo mmodzi wa achilamulo anayankha, nanena kwa Iye, Mphunzitsi, ndi kunena izi, mutitonza ifenso. Ndipo anati, Tsoka inunso, achilamulo inu! Chifukwa musenzetsa anthu akatundu osautsa ponyamula, ndipo inu nomwe simukhudza akatunduwo ndi chala chanu chimodzi. Tsoka inu! Chifukwa mumanga za pa manda a aneneri, ndipo makolo anu anawapha. Chomwecho muli mboni, ndipo muvomera ntchito za makolo anu; chifukwa iwotu anawapha, koma inu muwamangira iwo zapamanda. Mwa ichinso nzeru ya Mulungu inati, Ndidzatumiza kwa iwo aneneri ndi atumwi; ndipo ena a iwo adzawapha, nadzawazunza; kuti mwazi wa aneneri onse, wakhetsedwa kuyambira kukhazika kwa dziko lapansi, ukafunidwe kwa anthu a mbadwo uno; kuyambira mwazi wa Abele kufikira mwazi wa Zekariya, amene anamphera pakati pa guwa la nsembe ndi nyumba ya Kachisi. Indetu, ndinena kwa inu udzafunidwa kwa anthu a mbadwo uno. Tsoka inu, achilamulo! Chifukwa munachotsa chifungulo cha nzeru; inu simunalowamo nokha, ndipo munawaletsa iwo analinkulowa. Ndipo pamene Iye anatuluka m'menemo, alembi ndi Afarisi anayamba kumuumiriza Iye kolimba, ndi kumtompha Iye ndi zinthu zambiri; namlindira akakole kanthu kotuluka m'kamwa mwake. Pomwepo pamene anthu a zikwizikwi a khamu anasonkhana pamodzi, kotero kuti anapondana, Iye anayamba kunena kwa ophunzira ake poyamba, Tachenjerani nokha ndi chotupitsa mikate cha Afarisi, chimene chili chinyengo. Koma kulibe kanthu kovundikiridwa kamene sikadzaululidwa; ndi kobisika kamene sikadzadziwika. Chifukwa chake zonse zimene mwazinena mumdima zidzamveka poyera; ndipo chimene mwalankhula m'khutu, m'zipinda za m'kati chidzalalikidwa pa machindwi a nyumba. Ndipo ndinena kwa inu, abwenzi anga, Musaope iwo akupha thupi, ndipo akatha ichi alibe kanthu kena angathe kuchita. Koma ndidzakulangizani amene muzimuopa; taopani Iye amene atatha kupha ali ndi mphamvu yakutaya ku Gehena, inde, ndinena ndinu opani ameneyo. Kodi mpheta zisanu sizigulidwa timakobiri tiwiri? Ndipo palibe imodzi ya izo iiwalika pamaso pa Mulungu; komatu ngakhale matsitsi onse a pamutu panu awerengedwa. Musaopa, muposa mtengo wake wa mpheta zambiri. Ndipo ndinena kwa inu, Amene aliyense akavomereza Ine pamaso pa anthu, inde, Mwana wa Munthu adzamvomereza iye pamaso pa angelo a Mulungu; Koma iye wondikana Ine pamaso pa anthu, iye adzakanidwa pamaso pa angelo a Mulungu. Ndipo amene aliyense adzanenera Mwana wa Munthu zoipa adzakhululukidwa; koma amene anenera Mzimu Woyera zamwano sadzakhululukidwa. Ndipo pamene paliponse adzamuka nanu kumlandu wa m'sunagoge ndi kwa akulu, ndi aulamuliro, musade nkhawa ndi kuti mukadzikanira bwanji, ndipo ndi mau otani, kapena mukanena chiyani; pakuti Mzimu Woyera adzaphunzitsa inu nthawi yomweyo zimene muyenera kuzinena. Ndipo munthu wa m'khamulo anati kwa Iye, Mphunzitsi, uzani mbale wanga agawane ndi ine chuma chamasiye. Koma anati kwa iye, Munthu iwe, ndani anandiika Ine ndikhale woweruza, kapena wakugawira inu? Ndipo Iye anati kwa iwo, Yang'anirani, mudzisungire kupewa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo. Ndipo Iye ananena nao fanizo, kuti, Munda wake wa munthu mwini chuma unapatsa bwino. Ndipo anaganizaganiza mwa yekha nanena, Ndidzatani ine, popeza ndilibe mosungiramo zipatso zanga? Ndipo anati Ndidzatere: ndidzapasula nkhokwe zanga, ndi kumanganso zazikulu, ndipo ndidzasungiramo dzinthu zanga zonse, ndi chuma changa. Ndipo ndidzati kwa moyo wanga, Moyo iwe, uli nacho chuma chambiri chosungika kufikira zaka zambiri; tapumulatu, nudye, numwe, nukondwere. Koma Mulungu anati kwa iye, Wopusa iwe, usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako; ndipo zinthu zimene unazikonza zidzakhala za yani? Atero iye wakudziunjikira chuma mwini yekha wosakhala nacho chuma cha kwa Mulungu. Ndipo Iye anati kwa ophunzira ake, Chifukwa chake ndinena ndinu, Musade nkhawa ndi moyo wanu, chimene mudzadya; kapena ndi thupi lanu, chimene mudzavala. Pakuti moyo uli woposa chakudya, ndi thupi liposa chovala. Lingirirani makungubwi, kuti samafesai, kapena kutemai; alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu awadyetsa; nanga inu simuziposa mbalame kwambiri! Ndipo ndani wa inu, ndi kuda nkhawa angathe kuonjeza mkono pa msinkhu wake? Kotero ngati simungathe ngakhale chaching'onong'ono, muderanji nkhawa chifukwa cha zina zija? Lingalirani maluwa, makulidwe ao; sagwiritsa ntchito ndi kusapota; koma ndinena kwa inu, Ngakhale Solomoni, mu ulemerero wake wonse sanavale ngati limodzi la awa. Koma ngati Mulungu aveka kotere udzu wa kuthengo ukhala lero, ndipo mawa uponyedwa pamoto; nanga inu sadzakuninkhani koposa, inu okhulupirira pang'ono? Ndipo inu musafunefune chimene mudzadya, ndi chimene mudzamwa; ndipo musakayike mtima. Pakuti izi zonse mitundu ya anthu a pa dziko lapansi amazifunafuna; koma Atate wanu adziwa kuti musowa zimenezi. Komatu tafunafunani Ufumu wake, ndipo izi adzakuonjezerani. Musaopa, kagulu ka nkhosa inu; chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani Ufumu. Gulitsani zinthu muli nazo, nimupatse mphatso zachifundo; mudzikonzere matumba a ndalama amene sakutha, chuma chosatha m'Mwamba, kumene mbala siziyandikira, ndipo njenjete siziononga. Pakuti kumene kuli chuma chanu, komweko kudzakhalanso mtima wanu. Khalani odzimangira m'chuuno, ndipo nyali zanu zikhale zoyaka; ndipo inu nokha khalani ofanana ndi anthu oyembekezera mbuye wao, pamene ati abwera kuchokera kuukwati; kuti pakudza iye, nakagogoda, akamtsegulire pomwepo. Odala akapolowo amene mbuye wao, pakudza iye, adzawapeza odikira; indetu ndinena ndinu, kuti iye adzadzimangira m'chuuno, nadzawakhalitsa pansi kudya, nadzafika, nadzawatumikira. Ndipo akadza ulonda wachiwiri, kapena wachitatu, nakawapeza atero, odala amenewa. Koma zindikirani ichi, kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yake yakudza mbala, akadadikira, ndipo sakadalola nyumba yake ibooledwe. Khalani okonzeka inunso; chifukwa nthawi imene simulingirira, Mwana wa Munthu akudza. Ndipo Petro anati, Ambuye, kodi fanizo ili mwalinena kwa ife, kapena kwa onse? Ndipo Ambuye anati, Ndani tsono ali mdindo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake adzamuika kapitao wa pa banja lake, kuwapatsa iwo phoso lao pa nthawi yake? Wodala kapoloyo amene mbuye wake pakufika, adzampeza alikuchita chotero. Ndinena ndinu zoona, kuti adzamuika iye kapitao wa pa zonse ali nazo. Koma kapolo uyo akanena mumtima mwake, Mbuye wanga azengereza kudza; ndimo akayamba kupanda anyamata ndi adzakazi ndi kudya ndi kumwa, ndi kuledzera; mbuye wa kapolo uyo adzafika tsiku lakuti samuyembekezera, ndi nthawi yakuti saidziwa, nadzamdula iye pakati nadzamuika dera lake pamodzi ndi anthu osakhulupirira. Ndipo kapolo uyo, wodziwa chifuniro cha mbuye wake, ndipo sanakonza, ndi kusachita zonga za chifuniro chakecho, adzakwapulidwa mikwapulo yambiri. Koma iye amene sanachidziwe, ndipo anazichita zoyenera mikwapulo, adzakwapulidwa pang'ono. Ndipo kwa munthu aliyense adampatsa zambiri, kwa iye adzafuna zambiri; ndipo amene anamuikizira zambiri, adzamuuza abwezere zoposa. Ine ndinadzera kuponya moto pa dziko lapansi; ndipo ndifunanji ngati unatha kuyatsidwa? Koma ndili ndi ubatizo ndikabatizidwe nao; ndipo ndikanikizidwa Ine kufikira ukatsirizidwa! Kodi muyesa kuti ndinadzera kudzapatsa mtendere pa dziko lapansi? Ndinena kwa inu, Iaitu, komatu kutsutsana; pakuti kuyambira tsopano adzakhala m'nyumba imodzi anthu asanu, atatu adzatsutsana ndi awiri, ndi awiri adzatsutsana ndi atatu. Adzatsutsana atate ndi mwana wake, ndi mwana ndi atate wake; amake adzatsutsana ndi mwana wamkazi, ndi mwana wamkazi ndi amake, mpongozi adzatsutsana ndi mkazi wa mwana wake, ndi mkaziyo ndi mpongozi wake. Koma Iye ananenanso kwa makamu a anthu, Pamene paliponse muona mtambo wokwera kumadzulo, pomwepo munena, kuti, Ikudza mvula; ndipo itero. Ndipo pamene mphepo ya kumwera iomba, munena, kuti, Kudzakhala kutenthatu; ndipo kuterodi. Onyenga inu, mudziwa kuzindikira nkhope yake ya dziko lapansi ndi ya thambo; koma simudziwa bwanji kuzindikira nyengo yino? Ndipo inunso, pa nokha mulekeranji kuweruza kolungama? Pakuti pamene ulikupita naye mnzako wa mlandu kwa oweruza, fulumira panjira kutha naye mlandu, kuti angakokere iwe kwa oweruza, ndipo oweruzayo angapereke iwe kwa msilikali, ndi msilikali angaponye iwe m'nyumba yandende. Ine ndinena kwa iwe, Sudzatulukamo konse kufikira utalipira kakobiri kukumaliza. Ndipo anakhalako nthawi yomweyo, anthu ena amene anamuuza Iye za Agalileya, amene Pilato anasanganiza mwazi wao ndi nsembe zao. Ndipo Iye anayankha nati kwa iwo, Kodi muyesa kuti Agalileya aja anali anthu akuchimwa koposa Agalileya onse, chifukwa anamva zowawa izi? Ndinena kwa inu, Iaitu; koma ngati inu simutembenuka mtima, mudzaonongeka nonse momwemo. Kapena iwo aja khumi ndi asanu ndi atatu, amene nsanja yaitali ya m'Siloamu inawagwera, ndi kuwapha; kodi muyesa kuti iwo anali olakwa koposa anthu onse akukhala m'Yerusalemu? Ndinena kwa inu, Iaitu; koma ngati simutembenuka mtima, mudzaonongeka nonse chimodzimodzi. Ndipo Iye ananena fanizo ili: Munthu wina anali ndi mkuyu wooka m'munda wake wamphesa. Ndipo anadza nafuna chipatso pa uwu, koma anapeza palibe. Ndipo anati kwa wosungira munda wamphesa, Taona, zaka zapita zitatu ndimadza ine kudzafuna chipatso pa mkuyu uwu, ndipo ndimapeza palibe: taulikha; uyeseranjinso nthaka yopanda pake? Ndipo iye anayankha nanena naye, Mbuye, baulekani ngakhale chaka chino chomwe, kufikira ndidzaukumbira kwete, ndithirepo ndowe; ndipo ngati udzabala chipatso kuyambira pamenepo, chabwino; koma ngati iai, mudzaulikhatu. Ndipo analikuphunzitsa m'sunagoge mwina, tsiku la Sabata. Ndipo mkazi anali nao mzimu wakumdwalitsa zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu; nakhala wopeteka, ndimo analibe mphamvu konse yakuweramuka. Ndipo Yesu m'mene anamuona, anamuitana, nanena naye, Mkaziwe, wamasulidwa kudwala kwako. Ndipo anaika manja ake pa iye; ndipo pomwepo anaongoledwa, nalemekeza Mulungu. Ndipo mkulu wa sunagoge anavutika mtima, chifukwa Yesu anachiritsa tsiku la Sabata, nayankha, nanena kwa khamulo, Alipo masiku asanu ndi limodzi, m'menemo anthu ayenera kugwira ntchito, chifukwa chake idzani kudzachiritsidwa momwemo, koma tsiku la Sabata ai. Koma Ambuye anamyankha iye, nati, Onyenga inu, kodi munthu aliyense wa inu samaimasula ng'ombe yake, kapena bulu wake ku chodyeramo, tsiku la Sabata, kupita nayo kukaimwetsa madzi? Ndipo mkazi uyu, ndiye mwana wa Abrahamu, amene Satana anammanga, onani, zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu, nanga si kuyenera kodi, kuti amasulidwe nsinga yake imeneyi tsiku la Sabata? Ndipo pamene Iye anatero, onse aja akutsutsana naye ananyazitsidwa; ndipo anthu onse a m'khamu anakondwera ndi zinthu zonse za ulemererozo zinachitidwa ndi Iye. Pamenepo ananena, Ufumu wa Mulungu ufanana ndi chiyani? Ndipo ndidzaufanizira ndi chiyani? Ufanana ndi kambeu kampiru, kamene munthu anatenga, nakaponya m'munda wakewake, ndipo kanamera, kanakula mtengo; ndi mbalame za m'mlengalenga zinabindikira mu nthambi zake. Ndiponso anati, Ndidzafanizira Ufumu wa Mulungu ndi chiyani? Ufanana ndi chotupitsa mikate, chimene mkazi anatenga, nachibisa mu miyeso itatu ya ufa, kufikira unatupo wonsewo. Ndipo Iye anapita pakati pa mizinda ndi midzi, naphunzitsa, nayenda ulendo kunkabe ku Yerusalemu. Ndipo munthu anati kwa Iye, Ambuye, akupulumutsidwa ndiwo owerengeka kodi? Koma Iye anati kwa iwo, Yesetsani kulowa pa khomo lopapatiza; chifukwa anthu ambiri, ndikuuzani, adzafunafuna kulowamo, koma sadzakhoza. Pamene atauka mwini nyumba natseka pakhomo, ndipo inu mudzayamba kuima pabwalo, ndi kugogoda pachitseko, ndi kunena, Ambuye titsegulireni ife; ndipo Iye adzayankha nadzati ndi inu, Sindidziwa inu kumene muchokerako; pomwepo mudzayamba kunena, Ife tinadya ndi kumwa pamaso panu, ndipo munaphunzitsa m'makwalala a kwathu; ndipo Iye adzati, Ndinena kwa inu, sindidziwa kumene muchokera inu; chokani pa Ine, nonse akuchita chosalungama. Kudzakhala komweko kulira ndi kukukuta mano, pamene mudzaona Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, ndi aneneri onse, mu Ufumu wa Mulungu, koma inu nokha mutulutsidwa kunja. Ndipo anthu adzachokera kum'mawa, ndi kumadzulo, ndi kumpoto, ndi kumwera, nadzakhala pansi mu Ufumu wa Mulungu. Ndipo onani, alipo akuthungo amene adzakhala oyamba, ndipo alipo oyamba adzakhala akuthungo. Nthawi yomweyo anadzapo Afarisi ena, nanena kwa Iye, Tulukani, chokani kuno; chifukwa Herode afuna kupha Inu. Ndipo Iye anati kwa iwo, Pitani kauzeni nkhandweyo, Taonani, nditulutsa ziwanda, nditsiriza machiritso lero ndi mawa, ndipo mkucha nditsirizidwa. Komatu ndiyenera ndipite ulendo wanga lero ndi mawa ndi mkucha, chifukwa sikuloleka kuti mneneri aonongeke kunja kwake kwa Yerusalemu. Yerusalemu, Yerusalemu, iwe wakupha aneneri, ndi wakuponya miyala iwo atumidwa kwa iwe! Ha! Kawirikawiri ndinafuna kusonkhanitsa ana ako, monga ngati thadzi ndi anapiye ake m'mapiko ake, ndipo simunafunai! Onani nyumba yanu isiyidwa kwa inu yabwinja; ndipo ndinena kwa inu kuti, Simudzandiona Ine, kufikira mudzati, Wolemekezeka Iye amene akudza m'dzina la Ambuye. Ndipo panali pamene Iye analowa m'nyumba ya mmodzi wa akulu a Afarisi tsiku la Sabata, kukadya, iwo analikumzonda Iye. Ndipo onani, panali pamaso pake munthu wambulu. Ndipo Yesu anayankha nati kwa achilamulo ndi Afarisi, nanena, Kodi nkuloledwa tsiku la Sabata kuchiritsa, kapena iai? Koma iwo anakhala chete. Ndipo anamtenga namchiritsa, namuuza apite. Ndipo anati kwa iwo, Ndani wa inu bulu wake kapena ng'ombe yake itagwa m'chitsime, ndipo sadzaitulutsa pomwepo tsiku la Sabata kodi? Ndipo iwo sanathe kumbwezera mau pa zinthu izi. Ndipo Iye ananena fanizo kwa oitanidwa, popenya kuti amadzisankhira mipando yaulemu, nanena kwa iwo, Pamene paliponse waitanidwa iwe ndi munthu ku chakudya cha ukwati, usaseama pa mpando waulemu; kuti kapena wina waulemu wakuposa iwe akaitanidwe ndi iye, ndipo pakufika iye amene adaitana iwe ndi uyu, adzati kwa iwe, Mpatse uyu malo; ndipo pomwepo udzayamba manyazi kukhala pa mpando wa kuthungo. Koma pamene paliponse waitanidwa iwe, pita nukhale pansi pa malo a kuthungo; kotero kuti pamene akadza iye anakuitana iwe, akanena ndi iwe, Bwenzi langa, sendera, kwera kuno; pomwepo udzakhala ndi ulemerero pamaso pa onse akuseama pachakudya pamodzi ndi iwe. Chifukwa munthu aliyense wakudzikuza adzachepetsedwa; ndipo wakudzichepetsa adzakulitsidwa. Ndipo ananenanso kwa iye amene adamuitana, Pamene ukonza chakudya cha pausana kapena cha madzulo, usaitane abwenzi ako, kapena abale ako, kapena a fuko lako, kapena anansi ako eni chuma; kuti kapena iwonso angabwereze kuitana iwe, ndipo udzakhala nayo mphotho. Koma pamene ukonza phwando uitane aumphawi, opunduka, otsimphina, akhungu; ndipo udzakhala wodala; chifukwa iwo alibe chakubwezera iwe mphotho; pakuti idzabwezedwa mphotho pa kuuka kwa olungama. Ndipo pamene wina wa iwo akuseama pachakudya pamodzi ndi Iye anamva izi, anati kwa Iye, Wodala iye amene adzadya mkate mu Ufumu wa Mulungu. Koma anati kwa iye, Munthu wina anakonza phwando lalikulu; naitana anthu ambiri; ndipo anatumiza kapolo wake pa nthawi ya phwando kukanena kwa oitanidwawo, Idzani, chifukwa zonse zakonzeka tsopano. Ndipo onse ndi mtima umodzi anayamba kuwiringula. Woyamba anati kwa iye, Ine ndagula munda, ndipo ndiyenera ndituluke kukauona; ndikupempha undilole ine ndisafika. Ndipo anati wina, Ine ndagula ng'ombe za magoli asanu, ndipo ndinka kukaziyesa; ndikupempha undilole ine ndisafika. Ndipo anati wina, Ine ndakwatira mkazi, ndipo chifukwa chake sindingathe kudza. Ndipo kapoloyo pakubwera anauza mbuye wake zinthu izi. Pamenepo mwini nyumba anakwiya, nati kwa kapolo wake, Tuluka msanga, pita kumakwalala ndi kunjira za mudzi, nubwere nao muno aumphawi ndi opunduka ndi akhungu ndi otsimphina. Ndipo kapoloyo anati, Ambuye, chimene munachilamulira chachitika, ndipo malo atsalapo. Ndipo mbuye ananena kwa kapoloyo, Tuluka, nupite kumiseu ndi njira za kuminda, nuwaumirize anthu alowe, kuti nyumba yanga idzale. Pakuti ndinena kwa inu, kuti kulibe mmodzi wa amuna oitanidwa aja adzalawa phwando langa. Ndipo mipingo yambiri ya anthu inamuka naye; ndipo Iye anapotoloka, nati kwa iwo, Munthu akadza kwa Ine, wosada atate wake ndi amake, ndi mkazi wake, ndi ana, ndi abale, ndi alongo ake, inde ndi moyo wake womwe wa iye mwini, sakhoza kukhala wophunzira wanga. Ndipo amene aliyense sasenza mtanda wake wa mwini yekha, ndi kudza pambuyo panga, sakhoza kukhala wophunzira wanga. Pakuti ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sathanga wakhala pansi, nawerengera mtengo wake, aone ngati ali nazo zakuimaliza? Kuti kungachitike, pamene atakhazika pansi miyala ya kumaziko ake, osakhoza kuimaliza anthu onse akuyang'ana adzayamba kumseka iye, ndi kunena kuti, Munthu uyu anayamba kumanga, koma sanathe kumaliza. Kapena mfumu yanji pakupita kukomana ndi nkhondo ya mfumu inzake, sathanga wakhala pansi, nafunsana ndi akulu ngati akhoza ndi asilikali ake zikwi khumi kulimbana naye wina uja alikudza kukomana naye ndi asilikali zikwi makumi awiri? Koma ngati sakhoza, atumiza akazembe, pokhala winayo ali kutalitali, nafunsa za mtendere. Chifukwa chake tsono, yense wa inu amene sakaniza zonse ali nazo, sakhoza kukhala wophunzira wanga. Kotero mchere uli wokoma; koma ngati mchere utasukuluka adzaukoleretsa ndi chiyani? Suyenera kuuthira pamunda kapena padzala, autaya kunja. Amene ali nao makutu akumva amve. Koma amisonkho onse ndi anthu ochimwa analikumyandikira kudzamva Iye. Ndipo Afarisi ndi alembi anadandaula nati, Uyu alandira anthu ochimwa, nadya nao. Koma anati kwa iwo fanizo ili, nanena, Munthu ndani wa inu ali nazo nkhosa makumikhumi, ndipo pakutayika imodzi ya izo, sasiya nanga m'chipululu zinazo makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi zinai, nalondola yotayikayo kufikira aipeza? Ndipo pamene adaipeza, aisenza pa mapewa ake wokondwera. Ndipo pakufika kunyumba kwake amema abwenzi ake ndi anansi ake, nanena nao, Kondwerani ndi ine, chifukwa ndinapeza nkhosa yanga yotayikayo. Ndinena kwa inu, kotero kudzakhala chimwemwe Kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi wotembenuka mtima, koposa anthu olungama makumi asanu ndi anai mphambu asanu ndi anai, amene alibe kusowa kutembenuka mtima. Kapena mkazi wanji ali nazo ndalama zasiliva khumi, ngati itayika imodzi, sayatsa nyali, nasesa m'nyumba yake, nafunafuna chisamalire kufikira akaipeza? Ndipo m'mene aipeza amema abwenzi ake ndi anansi ake, nanena, Kondwerani ndi ine, chifukwa ndinapeza ndalama ndidatayayo. Chomwecho, ndinena kwa inu, kuli chimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa mmodzi amene atembenuka mtima. Ndipo Iye anati, Munthu wina anali ndi ana amuna awiri; ndipo wamng'onoyo anati kwa atate wake, Atate, ndigawirenitu zanga za pa chuma chanu. Ndipo iye anawagawira za moyo wake. Ndipo pakupita masiku owerengeka mwana wamng'onoyo anasonkhanitsa zonse, napita ulendo wake kudziko lakutali; ndipo komweko anamwaza chuma chake ndi makhalidwe a chitayiko. Ndipo pamene anatha zake zonse, panakhala njala yaikulu m'dziko muja, ndipo iye anayamba kusowa. Ndipo anamuka nadziphatikiza kwa mfumu imodzi ya dziko lija; ndipo uyu anamtumiza kubusa kwake kukaweta nkhumba. Ndipo analakalaka kukhutitsa mimba yake ndi makoko amene nkhumba zimadya, ndipo palibe munthu anamninkha kanthu. Koma m'mene anakumbukira mumtima, anati, Antchito olipidwa ambiri a atate wanga ali nacho chakudya chochuluka, ndipo ine ndionongeke kuno ndi njala? Ndidzanyamuka ndipite kwa atate wanga, ndipo ndidzanena naye, Atate, ndinachimwira Kumwamba ndi pamaso panu; sindiyeneranso konse kutchulidwa mwana wanu; mundiyese ine ngati mmodzi wa antchito anu. Ndipo iye ananyamuka, nadza kwa atate wake. Koma pakudza iye kutali atate wake anamuona, nagwidwa chifundo, nathamanga, namkupatira pakhosi pake, nampsompsonetsa. Ndipo mwanayo anati kwa iye, Atate ndinachimwira Kumwamba ndi pamaso panu, sindiyeneranso konse kutchulidwa mwana wanu. Koma atateyo ananena kwa akapolo ake, Tulutsani msanga mwinjiro wokometsetsa, nimumveke; ndipo mpatseni mphete kudzanja lake ndi nsapato kumapazi ake; ndipo idzani naye mwanawang'ombe wonenepa, mumuphe, ndipo tidye, tisekere; chifukwa mwana wanga uyu anali wakufa, ndipo akhalanso wamoyo; anali wotayika, ndipo wapezedwa. Ndipo anayamba kusekera. Koma mwana wake wamkulu anali kumunda. Ndipo pakubwera iye ndi kuyandikira kunyumba, anamva kuimba ndi kuvina. Ndipo anaitana mmodzi wa anyamata, namfunsa, Zinthu izi nzotani? Ndipo uyu anati kwa iye, Mng'ono wako wafika; ndipo atate wako anapha mwanawang'ombe wonenepa, chifukwa anamlandira iye wamoyo. Koma anakwiya, ndipo sanafune kulowamo. Ndipo atate wake anatuluka namdandaulira. Koma anayankha nati kwa atate wake, Onani, ine ndinakhala kapolo wanu zaka zambiri zotere, ndipo sindinalakwira lamulo lanu nthawi iliyonse; ndipo simunandipatsa ine kamodzi konse mwanawambuzi, kuti ndisekere ndi abwenzi anga. Koma pamene anadza mwana wanu uyu, wakutha zamoyo zanu ndi akazi achiwerewere, munamphera iye mwanawang'ombe wonenepa. Koma iye ananena naye, Mwana wanga, iwe uli ndine nthawi zonse, ndipo zanga zonse zili zako. Koma kudayenera kuti tisangalale ndi kukondwerera: chifukwa mng'ono wako uyu anali wakufa ndipo ali ndi moyo; anatayika, ndipo wapezeka. Ndipo Iye ananenanso kwa ophunzira ake, Panali munthu mwini chuma, anali ndi kapitao wake; ndipo ameneyu ananenezedwa kwa iye kuti alikumwaza chuma chake. Ndipo anamuitana, nati kwa iye, Ichi ndi chiyani ndikumva za iwe? Undiwerengere za ukapitao wako; pakuti sungathe kukhalabe kapitao. Ndipo kapitao uyu anati mumtima mwake, Ndidzachita chiyani, chifukwa mbuye wanga andichotsera ukapitao? Kulima ndilibe mphamvu, kupemphapempha kundichititsa manyazi. Ndidziwa chimene ndidzachita, kotero kuti pamene ananditulutsa muukapitao, anthu akandilandire kunyumba kwao. Ndipo anadziitanira mmodzi ndi mmodzi amangawa onse a mbuye wake, nanena kwa woyamba, Unakongola chiyani kwa mbuye wanga? Ndipo anati, Mitsuko ya mafuta zana. Ndipo iye ananena naye, Tenga kalata wako, nukhale pansi msanga, nulembere, Makumi asanu. Pomwepo anati kwa wina, Ndipo iwe uli nao mangawa otani? Ndipo uyu anati, Madengu a tirigu zana. Iye ananena naye, Tenga kalata wako nulembere makumi asanu ndi atatu. Ndipo mbuye wake anatama kapitao wonyengayo, kuti anachita mwanzeru; chifukwa ana a nthawi ya pansi pano ali anzeru m'mbadwo wao koposa ana a kuunika. Ndipo Ine ndinena kwa inu, Mudziyesere nokha abwenzi ndi chuma chosalungama; kuti pamene chikakusowani, iwo akalandire inu m'mahema osatha. Iye amene akhulupirika m'chaching'onong'ono alinso wokhulupirika m'chachikulu; ndipo iye amene ali wosalungama m'chachikulu. Chifukwa chake ngati simunakhala okhulupirika m'chuma cha chosalungama, adzakhulupirira inu ndani ndi chuma choona? Ndipo ngati simunakhala okhulupirika ndi zake za wina, adzakupatsani inu ndani za inu eni? Palibe mnyamata wa m'nyumba akhoza kukhala kapolo wa ambuye awiri; pakuti kapena adzamuda wina, nadzakonda winayo; kapena adzatsata wina, nadzapeputsa winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma. Koma Afarisi, ndiwo okonda ndalama, anamva izi zonse; ndipo anamseka. Ndipo anati kwa iwo, Inu ndinu odziyesera nokha olungama pamaso pa anthu; koma Mulungu azindikira mitima yanu; chifukwa ichi chimene chikuzika mwa anthu chili chonyansa pamaso pa Mulungu. Chilamulo ndi aneneri analipo kufikira pa Yohane; kuyambira pamenepo ulalikidwa Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndipo munthu aliyense akangamira kulowamo. Kuti kumwamba ndi dziko lapansi zichoke nkwapafupi, koma kuti kalembo kakang'ono kachilamulo kagwe nkwapatali. Yense wakusudzula mkazi wake, nakwatira wina, achita chigololo; ndipo iye amene akwatira wosudzulidwayo, achita chigololo. Ndipo panali munthu mwini chuma amavala chibakuwa ndi nsalu yabafuta, nasekera, nadyerera masiku onse; ndipo wopemphapempha wina, dzina lake Lazaro, adaikidwa pakhomo pake wodzala ndi zilonda, ndipo anafuna kukhuta ndi zakugwa pa gome la mwini chumayo; komatu agalunso anadza nanyambita zilonda zake. Ndipo kunali kuti wopemphayo adafa, ndi kuti anatengedwa iye ndi angelo kunka kuchifuwa cha Abrahamu; ndipo mwini chumayo adafanso, naikidwa m'manda. Ndipo m'dziko la akufa anakweza maso ake, pokhala nao mazunzo, naona Abrahamu patali, ndi Lazaro m'chifuwa mwake. Ndipo anakweza mau nati, Atate Abrahamu, mundichitire chifundo, mutume Lazaro, kuti aviike nsonga ya chala chake m'madzi, naziziritse lilime langa; pakuti ndizunzidwadi m'lawi ili la moto. Koma Abrahamu anati, Mwana, kumbukira kuti unalandira zokoma zako pakukhala m'moyo iwe, momwemonso Lazaro zoipa; ndipo tsopano iye asangalatsidwa pano, koma iwe uzunzidwadi. Ndipo pamwamba pa izi, pakati pa ife ndi inu pakhazikika phompho lalikulu, kotero kuti iwo akufuna kuoloka kuchokera kuno kunka kwa inu sangathe, kapena kuchokera kwanuko kuyambuka kudza kwa ife, sangathenso. Koma anati, Pamenepo ndikupemphani, Atate, kuti mumtume kunyumba ya atate wanga; pakuti ndili nao abale asanu; awachitire umboni iwo kuti iwonso angadze kumalo ano a mazunzo. Koma Abrahamu anati, Ali ndi Mose ndi aneneri; amvere iwo. Koma anati, Iai, Atate Abrahamu, komatu ngati wina akapita kwa iwo wochokera kwa kufa adzasandulika mtima. Koma anati kwa iye, Ngati samvera Mose ndi aneneri, sadzakopeka mtima ngakhale wina akauka kwa akufa. Ndipo anati kwa ophunzira ake, Sikutheka kuti zolakwitsa zisadze; koma tsoka iye amene adza nazo. Kukolowekedwa mwala wamphero m'khosi mwake ndi kuponyedwa iye m'nyanja nkwapafupi, koma kulakwitsa mmodzi wa ang'ono awa nkwapatali. Kadzichenjerani nokha; akachimwa mbale wako umdzudzule, akalapa, umkhululukire. Ndipo akakuchimwira kasanu ndi kawiri pa tsiku lake, nakakutembenukira kasanu ndi kawiri ndi kunena, Ndalapa ine; uzimkhululukira. Ndipo atumwi anati kwa Ambuye, Mutionjezere chikhulupiriro. Koma Ambuye anati, Mukakhala nacho chikhulupiriro ngati kambeu kampiru, mukanena kwa mtengo uwu wamkuyu, Uzulidwe, nuokedwe m'nyanja; ndipo ukadamvera inu. Koma ndani mwa inu ali naye kapolo wolima, kapena woweta nkhosa, amene pobwera iye kuchokera kumunda adzanena kwa iye, Lowa tsopano, khala pansi kudya; wosanena naye makamaka, Undikonzere chakudya ine, nudzimangire, nunditumikire kufikira ndadya ndi kumwa; ndipo nditatha ine udzadya nudzamwa iwe? Kodi ayamika kapoloyo chifukwa anachita zolamulidwa? Chotero inunso m'mene mutachita zonse anakulamulirani, nenani, Ife ndife akapolo opanda pake, tangochita zimene tayenera kuzichita. Ndipo kunali, pakumuka ku Yerusalemu Iye analikupita pakati pa Samariya ndi Galileya. Ndipo m'mene analowa Iye m'mudzi wina, anakomana naye amuna khumi akhate, amene anaima kutali; ndipo iwo anakweza mau, nanena, Yesu, Mbuye, mutichitire chifundo. Ndipo pakuwaona anati kwa iwo, Pitani, kadzionetseni nokha kwa ansembe. Ndipo kunali, m'kumuka kwao, anakonzedwa. Ndipo mmodzi wa iwo, pakuona kuti anachiritsidwa, anabwerera m'mbuyo, nalemekeza Mulungu ndi mau akulu; ndipo anagwa nkhope yake pansi kumapazi ake, namyamika Iye; ndipo anali Msamariya ameneyo. Ndipo Yesu anayankha nati, Kodi sanakonzedwe khumi? Koma ali kuti asanu ndi anai aja? Akubwera kulemekeza Mulungu sanapezeka mmodzi kodi, koma mlendo uyu? Ndipo anati kwa iye, Nyamuka, nupite; chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe. Ndipo pamene Afarisi anamfunsa Iye, kuti, Ufumu wa Mulungu ukudza liti, anawayankha, nati, Ufumu wa Mulungu sukudza ndi maonekedwe; ndipo sadzanena, Taonani uwu, kapena uwo! Pakuti, taonani, Ufumu wa Mulungu uli m'kati mwa inu. Ndipo anati kwa ophunzira ake, Adzadza masiku, amene mudzakhumba kuona limodzi la masiku a Mwana wa Munthu, koma simudzaliona. Ndipo adzanena ndi inu, Taonani ilo! Taonani ili? Musachoka kapena kuwatsata; pakuti monga mphezi ing'anipa kuchokera kwina pansi pa thambo, niunikira kufikira kwina pansi pa thambo, kotero adzakhala Mwana wa Munthu m'tsiku lake. Koma ayenera athange wamva zowawa zambiri nakanidwe ndi mbadwo uno. Ndipo monga kunakhala masiku a Nowa, momwemo kudzakhalanso masiku a Mwana wa Munthu. Anadya, anamwa, anakwatira, anakwatiwa, kufikira tsiku lija Nowa analowa m'chingalawa, ndipo chinadza chigumula, nichiwaononga onsewo. Monga momwenso kunakhala masiku a Loti; anadya, anamwa, anagula, anagulitsa, anabzala, anamanga nyumba; koma tsiku limene Loti anatuluka m'Sodomu udavumba moto ndi sulufure zochokera kumwamba, ndipo zinawaononga onsewo; momwemo kudzakhala tsiku lakuvumbuluka Mwana wa Munthu. Tsikulo iye amene adzakhala pamwamba pa chindwi, ndi akatundu ake m'nyumba, asatsike kuwatenga; ndipo iye amene ali m'munda modzimodzi asabwere ku zake za m'mbuyo. Kumbukirani mkazi wa Loti. Iye aliyense akafuna kusunga moyo wake adzautaya, koma iye aliyense akautaya, adzausunga. Ndinena ndi inu, usiku womwewo adzakhala awiri pa kama mmodzi; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa. Padzakhala akazi awiri akupera pamodzi, mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa. *** Ndipo anayankha nanena kwa Iye, Kuti, Ambuye? Ndipo anati kwa iwo, Pamene pali mtembo, pomweponso miimba idzasonkhanidwa. Ndipo anawanenera fanizo lakuti ayenera iwo kupemphera nthawi zonse, osafooka mtima; nanena, M'mudzi mwakuti munali woweruza wosaopa Mulungu, ndi wosasamala munthu. Ndipo m'mudzimo munali mkazi wamasiye; ndipo anadza kwa iye nanena, Mundiweruzire mlandu pa wotsutsana nane. Ndipo sanafune nthawi; koma bwinobwino anati mwa yekha, Ndingakhale sindiopa Mulungu kapena kusamala munthu; koma chifukwa cha kundivuta ine mkazi wamasiye amene ndidzamweruzira mlandu, kuti angandilemetse ndi kudzaidza kwake. Ndipo Ambuye anati, Tamverani chonena woweruza wosalungama. Ndipo kodi Mulungu sadzachitira chilungamo osankhidwa ake akumuitana usana ndi usiku, popeza aleza nao mtima? Ndinena ndi inu, adzawachitira chilungamo posachedwa. Koma Mwana wa Munthu pakudza Iye, adzapeza chikhulupiriro pa dziko lapansi kodi? Ndipo anatinso kwa ena amene anadzikhulupirira mwa iwo okha kuti ali olungama, napeputsa onse ena, fanizo ili, Anthu awiri anakwera kunka ku Kachisi kukapemphera; winayo Mfarisi ndi mnzake wamsonkho. Mfarisiyo anaimirira napemphera izi mwa yekha, Mulungu, ndikuyamikani kuti sindili monga anthu onse ena, opambapamba, osalungama, achigololo, kapenanso monga wamsonkho uyu; ndisala chakudya kawiri sabata limodzi; ndipereka limodzi la magawo khumi la zonse ndili nazo. Koma wamsonkhoyo alikuima patali sanafune kungakhale kukweza maso kumwamba, komatu anadziguguda pachifuwa pake nanena, Mulungu, mundichitire chifundo, ine wochimwa. Ndinena ndi inu, anatsikira kunyumba kwake woyesedwa wolungama uyutu, wosati uja ai; pakuti yense wakudzikuza yekha adzachepetsedwa; koma wodzichepetsa yekha adzakulitsidwa. Ndipo anadza nao kwa Iye ana amakanda kuti awakhudze; koma pamene ophunzira anaona anawadzudzula. Koma Yesu anawaitana, nanena, Lolani ana adze kwa Ine, ndipo musawaletse; pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa otere. Indetu ndinena kwa inu, Aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana, sadzalowamo ndithu. Ndipo mkulu wina anamfunsa Iye, nanena, Mphunzitsi wabwino, ndizichita chiyani, kuti ndilowe moyo wosatha? Koma Yesu anati kwa iye, Unditcha Ine wabwino bwanji? Palibe wabwino, koma mmodzi, ndiye Mulungu. Udziwa malamulo. Usachite chigololo, Usaphe, Usabe, Usachite umboni wonama, Lemekeza atate wako ndi amai ako. Koma anati, Izi zonse ndazisunga kuyambira ubwana wanga. Koma m'mene Yesu anamva, anati kwa iye, Usowa chinthu chimodzi: gulitsa zilizonse uli nazo, nugawire osauka; ndipo udzakhala nacho chuma chenicheni m'Mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine. Koma pakumva izi anagwidwa nacho chisoni chambiri; pakuti anali mwini chuma chambiri. Ndipo Yesu pomuona iye anati, Ha! Nkuvutika nanga kwa anthu eni chuma kulowa Ufumu wa Mulungu! Pakuti nkwapafupi kwa ngamira ipyole diso la singano koma kwa munthu mwini chuma, kulowa Ufumu wa Mulungu nkwapatali. Koma akumvawo anati, Tsono ndani angathe kupulumutsidwa? Koma Iye anati, Zinthu zosatheka ndi anthu zitheka ndi Mulungu. Ndipo Petro anati, Taonani ife tasiya zathu za ife eni, ndipo takutsatani Inu. Koma anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Palibe munthu wasiya nyumba, kapena mkazi, kapena abale, kapena akum'bala, kapena ana, chifukwa cha Ufumu wa Mulungu, koma adzalandira zobwezedwa koposatu m'nthawi yino; ndipo m'nthawi ilinkudza moyo wosatha. Ndipo anadzitengera khumi ndi awiriwo, nati kwa iwo, Taonani, tikwera kunka ku Yerusalemu, ndipo zidzakwaniritsidwa kwa Mwana wa Munthu zonse zolembedwa ndi aneneri. Pakuti adzampereka kwa amitundu, nadzamseka, nadzamchitira chipongwe, nadzamthira malovu; ndipo atamkwapula adzamupha Iye; ndipo tsiku lachitatu adzauka. Ndipo sanadziwitse kanthu ka izi; ndi mau awa adawabisikira, ndipo sanazindikire zonenedwazo. Ndipo kunali, pamene anayandikira ku Yeriko, msaona wina anakhala m'mbali mwa njira, napemphapempha; ndipo pakumva khamu la anthu alinkupita, anafunsa, Ichi nchiyani? Ndipo anamuuza iye, kuti, Yesu Mnazarayo alinkupita. Ndipo anafuula, nanena, Yesu, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo. Ndipo iwo akutsogolera anamdzudzula iye, kuti akhale chete; koma iye anafuulitsa chifuulire, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo. Ndipo Yesu anaima, nalamulira kuti abwere naye kwa Iye; ndipo m'mene adafika pafupi, anamfunsa iye, Ufuna ndikuchitire chiyani? Ndipo anati, Ambuye, kuti ndipenyenso. Ndipo Yesu anati kwa iye, Penyanso: chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe. Ndipo pomwepo anapenyanso, namtsata Iye, ndi kulemekeza Mulungu: ndipo anthu onse pakuona, anachitira Mulungu mayamiko. Ndipo analowa, napyola pa Yeriko. Ndipo taonani, mwamuna wotchedwa dzina lake Zakeyo; ndipo iye anali mkulu wa amisonkho, nali wachuma. Ndipo anafuna kuona Yesu ndiye uti, ndipo sanathe, chifukwa cha khamulo, pakuti anali wamfupi msinkhu. Ndipo anathamanga, natsogola, nakwera mumkuyu kukamuona Iye; pakuti anati apite njira yomweyi. Ndipo m'mene anadza pamalopo Yesu anakweza maso nati kwa iye, Zakeyo, fulumira, nutsike; pakuti lero ndiyenera kukhala m'nyumba mwako. Ndipo anafulumira, natsika, namlandira Iye wokondwera. Ndipo m'mene anachiona anadandaula onse, nanena, Analowa amchereze munthu ali wochimwa. Ndipo Zakeyo anaimirira nati kwa Ambuye, Taonani, Ambuye, gawo limodzi la zanga zonse zogawika pakati ndipatsa osauka; ndipo ngati ndalanda kanthu kwa munthu monyenga, ndimbwezera kanai. Ndipo Yesu anati kwa iye, Lero chipulumutso chagwera nyumba iyi, popeza iyenso ndiye mwana wa Abrahamu. Pakuti Mwana wa Munthu anadza kufunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho. Ndipo pakumva izi iwo, Iye anaonjeza nanena fanizo, chifukwa anali Iye pafupi pa Yerusalemu, ndipo iwo anayesa kuti Ufumu wa Mulungu ukuti uonekere pomwepo. Pamenepo anati, Munthu wa fuko lomveka ananka kudziko lakutali, kudzilandirira yekha ufumu, ndi kubwerako. Ndipo anaitana akapolo ake khumi, nawapatsa iwo ndalama khumi za mina, nati kwaiwo, Chita nazoni malonda kufikira ndibweranso. Koma mfulu za pamudzi pake zinamuda, nizituma akazembe amtsate m'mbuyo ndi kunena, Ife sitifuna munthuyo akhale mfumu yathu. Ndipo kunali, pakubwera iye, atalandira ufumuwo, anati aitanidwe kwa iye akapolo aja, amene adawapatsa ndalamazo, kuti adziwe umo anapindulira pochita malonda. Ndipo anafika woyamba, nanena, Mbuye, mina yanu inachita nionjeza mina khumi. Ndipo anati kwa iye, Chabwino, kapolo wabwino iwe; popeza unakhala wokhulupirika m'chaching'onong'ono, khala nao ulamuliro pa midzi khumi. Ndipo anadza wachiwiri, nanena, Mbuye, mina yanu yapindula mina zisanu. Ndipo anati kwa iyenso, Khala iwenso woweruza midzi isanu. Ndipo wina anadza, nanena, Mbuye, taonani, siyi mina yanu, ndaisunga m'kansalu; pakuti ndinakuopani, popeza inu ndinu munthu wouma mtima: munyamula chimene simunachiika pansi, mututa chimene simunachifesa. Ananena kwa iye, Pakamwa pako ndikuweruza, kapolo woipa iwe. Unadziwa kuti ine ndine munthu wouma mtima, wonyamula chimene sindinachiika, ndi wotuta chimene sindinachifesa; ndipo sunapereka bwanji ndalama yanga pokongoletsa, ndipo ine pakudza ndikadaitenga ndi phindu lake? Ndipo anati kwa iwo akuimirirapo, Mchotsereni minayo, nimuipatse kwa iye wakukhala nazo mina khumi. Ndipo anati kwa iye, Mbuye, ali nazo mina khumi. Ndinena ndi inu, kuti kwa yense wakukhala nacho kudzapatsidwa; koma kwa iye amene alibe kanthu, chingakhale chimene ali nacho chidzachotsedwa. Koma adani anga aja osafuna kuti ndidzakhala mfumu yao, bwerani nao kuno, nimuwaphe pamaso panga. Ndipo m'mene adanena izi anawatsogolera nakwera ku Yerusalemu. Ndipo kunali, m'mene anayandikira ku Betefage ndi Betaniya, pa phiri lotchedwa la Azitona, anatuma awiri a ophunzira, nati, Mukani kumudzi uli pandunji panu; m'menemo, polowa, mudzapeza mwana wa bulu womangidwa, pamenepo palibe munthu anakwerapo nthawi iliyonse; mummasule iye nimumtenge. Ndipo munthu akati kwa inu, Mummasuliranji? Mudzatero naye, Ambuye amfuna iye. Ndipo anachoka otumidwawo, napeza monga adanena kwa iwo. Ndipo pamene anamasula mwana wa bulu, eni ake anati kwa iwo, Mumasuliranji mwana wa bulu? Ndipo anati, Ambuye amfuna iye. Ndipo anadza naye kwa Yesu; ndipo anayalika zovala zao pa mwana wa buluyo, nakwezapo Yesu. Ndipo pakupita Iye, anayala zovala zao m'njira. Ndipo pakuyandikira Iye tsono potsetsereka pake pa phiri la Azitona, unyinji wonse wa ophunzira anayamba kukondwera ndi kuyamika Mulungu ndi mau akulu, chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu anaziona; nanena, Wolemekezeka Mfumuyo ikudza m'dzina la Ambuye; mtendere m'Mwamba, ndi ulemerero m'Mwambamwamba. Ndipo Afarisi ena a m'khamu la anthu anati kwa Iye, Mphunzitsi, dzudzulani ophunzira anu. Ndipo anayankha nati, Ndinena ndi inu, ngati awa khala chete miyala idzafuula. Ndipo m'mene anayandikira, anaona mudziwo naulirira, nanena, Ukadazindikira tsiku ili, inde iwetu zinthu za mtendere! Koma tsopano zibisika pamaso pako. Pakuti masiku adzakudzera, ndipo adani ako adzakuzingira linga, nadzakuzungulira iwe kwete, nadzakutsekereza ponsepo; ndipo adzakupasula iwe, ndi ana ako mwa iwe; ndipo sadzasiya mwa iwe mwala wina pa mwala unzake; popeza sunazindikira nyengo ya mayang'aniridwe ako. Ndipo analowa m'Kachisi, nayamba kutulutsa iwo akugulitsa malonda, nanena nao, Kwalembedwa, Ndipo nyumba yanga idzakhala nyumba yakupemphera; koma inu mwaiyesa phanga la achifwamba. Ndipo analikuphunzitsa m'Kachisi tsiku ndi tsiku. Koma ansembe aakulu, ndi alembi ndi akulu a anthu anafunafuna kumuononga Iye; ndipo sanapeze chimene akachita; pakuti anthu onse anamlendewera Iye kuti amve. Ndipo kunali lina la masiku ao m'mene Iye analikuphunzitsa anthu m'Kachisi, ndi kulalikira Uthenga Wabwino, adamdzera ansembe aakulu ndi alembi pamodzi ndi akulu; ndipo anati, nanena naye, Mutiuze muchita izi ndi ulamuliro wotani? Kapena ndani iye amene anakupatsani ulamuliro umene? Ndipo anayankha, nati kwa iwo, Ndidzakufunsani mau Inenso; mundiuze: Ubatizo wa Yohane unachokera Kumwamba kodi, kapena kwa anthu? Ndipo anatsutsana mwa okha, nanena, Ngati tinena uchokera Kumwamba; adzati, Simunamkhulupirira chifukwa ninji? Ndiponso, tikanena, Uchokera kwa anthu; anthu onse adzatiponya miyala: pakuti akopeka mtima, kuti Yohane ali mneneri. Ndipo anayankha kuti sadziwa kumene uchokera. Ndipo Yesu anati kwa iwo Ndingakhale Inenso sindikuuzani ulamuliro umene ndichita nao zinthu izi. Ndipo Iye anayamba kunena kwa anthu fanizo ili: Munthu analima munda wamphesa, naukongoletsa kwa olima munda, nanka kudziko lina, nagonerako nthawi yaikulu. Ndipo pa nyengo ya zipatso anatumiza kapolo wake kwa olima mundawo, kuti ampatseko chipatso cha mundawo; koma olimawo anampanda, nambweza wopanda kanthu. Ndipo anatumizanso kapolo wina; ndipo iyenso anampanda, namchitira chipongwe, nambweza, wopanda kanthu. Ndipo anatumizanso wina wachitatu; ndipo iyenso anamlasa, namtaya kunja. Ndipo mwini mundawo anati, Ndidzachita chiyani? Ndidzatuma mwana wanga amene ndikondana naye; kapena akamchitira iye ulemu. Koma olimawo, pamene anamuona, anauzana wina ndi mnzake, nati, Uyu ndiye wolowa nyumba; tiyeni timuphe, kuti cholowa chake chikhale chathu. Ndipo anamponya kunja kwa mundawo, namupha. Pamenepo mwini munda wamphesawo adzawachitira chiyani? Iye adzafika nadzaononga olima munda aja, nadzapatsa munda kwa ena. Ndipo pamene iwo anamva, anati, Musatero iai! Koma Iye anawapenyetsa iwo, nati, Nchiyani ichi chinalembedwa, Mwala umene anaukana omanga nyumba, womwewu unakhala mutu wa pangodya. Munthu yense wakugwa pa mwala uwu, adzaphwanyika; koma iye amene udzamgwera, udzamupha. Ndipo alembi ndi ansembe aakulu anafunafuna kumgwira ndi manja nthawi yomweyo; ndipo anaopa anthu; pakuti anazindikira kuti ananenera pa iwo fanizo ili. Ndipo anamyang'anira, natumiza ozonda, amene anadzionetsera ngati olungama mtima, kuti akamkole pa mau ake, kotero kuti akampereke Iye ku ukulu ndi ulamuliro wa kazembe. Ndipo anamfunsa Iye, nanena, Mphunzitsi, ife tidziwa kuti munena ndi kuphunzitsa kolunjika, ndi kusasamalira nkhope ya munthu, koma muphunzitsa njira ya Mulungu koonadi; kodi kuloledwa kupereka msonkho kwa Kaisara, kapena iai? Koma Iye anazindikira chinyengo chao, nati kwa iwo, Tandionetsani Ine rupiya latheka. Chithunzithunzi ndi cholemba chake ncha yani? Anati iwo, Cha Kaisara. Ndipo Iye anati kwa iwo, Chifukwa chake perekani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu. Ndipo sanakhoze kugwira mauwo pamaso pa anthu; ndipo anazizwa ndi kuyankha kwake, nakhala chete. Ndipo anadza kwa Iye Asaduki ena, amene amanena kuti palibe kuuka kwa akufa; ndipo anamfunsa Iye, nanena, Mphunzitsi, Mose anatilembera ife, kuti mbale wake wa munthu akafa, wokhala ndi mkazi, ndipo alibe mwana iye, mbale wake adzakwatira mkaziyo, nadzamuukitsira mbale wake mbeu. Tsono panali abale asanu ndi awiri; ndipo woyamba anakwatira mkazi, nafa wopanda mwana; ndipo wachiwiri, ndi wachitatu anamtenga mkaziyo; ndipo choteronso asanu ndi awiri onse, sanasiye mwana, namwalira. Pomalizira anamwaliranso mkaziyo. Potero m'kuuka iye adzakhala mkazi wa yani wa iwo? Pakuti asanu ndi awiriwo adamkwatira iye. Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ana a dziko lapansi akwatira nakwatiwa: koma iwo akuyesedwa oyenera kufikira dziko lijalo, ndi kuuka kwa akufa, sakwatira kapena kukwatiwa. Pakuti sangathe kufanso nthawi zonse; pakuti afanafana ndi angelo; ndipo ali ana a Mulungu, popeza akhala ana a kuuka kwa akufa. Koma za kuti anthu akufa auka, anasonyeza ngakhale Mose, pa Chitsamba chija, pamene iye amtchulira Ambuye, Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo. Ndipo Iye sakhala Mulungu wa akufa, koma wa amoyo: pakuti anthu onse akhala ndi moyo kwa Iye. Ndipo alembi ena anayankha nati, Mphunzitsi, mwanena bwino. Pakuti sanalimbenso mtima kumfunsa Iye kanthu kena. Koma Iye anati kwa iwo, Amanena bwanji kuti Khristuyo ndiye mwana wa Davide? Pakuti Davide yekha anena m'buku la Masalmo, Ambuye ananena kwa Ambuye wanga, ukhale pa dzanja langa lamanja, kufikira Ine ndikaika adani ako pansi pa mapazi ako. Chotero Davide anamtchula Iye Ambuye, ndipo nanga ali mwana wake bwanji? Ndipo pamene anthu onse analinkumva Iye, anati kwa ophunzira, Chenjerani nao alembi, amene afuna kuyendayenda ovala miinjiro, nakonda kupatsidwa moni m'misika, ndi mipando yaulemu m'sunagoge, ndi malo aulemu pamaphwando; amene aononga nyumba za akazi amasiye, ndipo monyenga achita mapemphero atali; amenewo adzalandira kulanga koposa. Ndipo Yesu anakweza maso, naona anthu eni chuma alikuika zopereka zao mosungiramo ndalama. Ndipo anaona mkazi wina wamasiye waumphawi alikuika momwemo timakobiri tiwiri. Ndipo Iye anati, Zoonadi ndinena kwa inu, wamasiye uyu waumphawi anaikamo koposa onse; pakuti onse amenewa anaika mwa unyinji wao pa zoperekazo; koma iye mwa kusowa kwake anaikamo za moyo wake, zonse anali nazo. Ndipo pamene ena analikunena za Kachisiyo, kuti anakonzeka ndi miyala yokoma ndi zopereka, anati Iye, Zinthu izi muziona, adzafika masiku, pamenepo sudzasiyidwa pano mwala pa mwala unzake, umene sudzagwetsedwa. Ndipo iwo anamfunsa Iye, nati, Mphunzitsi, nanga zinthu izi zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro ndi chiyani pamene izi ziti zichitike? Ndipo Iye anati, Yang'anirani musasocheretsedwe; pakuti ambiri adzadza m'dzina langa, nadzanena, Ndine amene; ndipo, Nthawi yayandikira; musawatsate pambuyo pao. Ndipo pamene mudzamva za nkhondo ndi mapanduko, musaopsedwa; pakuti ziyenera izi ziyambe kuchitika; koma mathedwe sakhala pomwepo. Pamenepo ananena nao, Mtundu wa anthu udzaukira pa mtundu wina, ndipo ufumu pa ufumu wina: ndipo kudzakhala zivomezi zazikulu, ndi njala ndi miliri m'malo akutiakuti, ndipo kudzakhala zoopsa ndi zizindikiro zazikulu zakumwamba. Koma zisanachitike izi, anthu adzakuthirani manja, nadzakuzunzani, nadzapereka inu ku masunagoge ndi ndende, nadzamuka nanu kwa mafumu ndi akazembe, chifukwa cha dzina langa. Kudzakhala kwa inu ngati umboni. Chifukwa chake tsimikizani mumtima mwanu, kuti usanafike mlandu musalingirire chimene mudzayankha. Pakuti Ine ndidzakupatsani inu kamwa ndi nzeru, zimene adani anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa. Koma mudzaperekedwa ngakhale ndi akukubalani, ndi abale, ndi a fuko lanu, ndi abwenzi anu; ndipo ena a inu adzakuphani. Ndipo anthu onse adzadana ndi inu chifukwa cha dzina langa. Ndipo silidzaonongeka tsitsi limodzi la pamutu panu. Mudzakhala nao moyo wanu m'chipiriro. Koma pamene paliponse mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti chipulumutso chake chayandikira. Pamenepo iwo ali m'Yudeya athawire kumapiri, ndi iwo ali m'kati mwa uwo atuluke, ndi iwo ali kumilaga asalowemo. Chifukwa amenewa ndi masiku akubwezera, kuti zonse zidalembedwa zichitike. Koma tsoka iwo akukhala ndi pakati, ndi iwo akuyamwitsa ana masiku awo! Pakuti padzakhala chisauko chachikulu padziko, ndi mkwiyo pa anthu awa. Ndipo adzagwa ndi lupanga lakuthwa, nadzagwidwa ndende kunka kumitundu yonse ya anthu; ndipo mapazi a anthu akunja adzapondereza Yerusalemu kufikira kuti nthawi zao za anthu akunja zakwanira. Ndipo kudzakhala zizindikiro pa dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi; ndi pa dziko lapansi chisauko cha mitundu ya anthu, alikuthedwa nzeru pa mkukumo wake wa nyanja ndi mafunde ake; anthu akukomoka ndi mantha, ndi kuyembekezera zinthu zilinkudza kudziko lapansi; pakuti mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka. Ndipo pamenepo adzaona Mwana wa Munthu alinkudza mu mtambo ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu. Koma poyamba kuchitika izi weramukani, tukulani mitu yanu; chifukwa chiomboledwe chanu chayandikira. Ndipo ananena nao fanizo; Onani mkuyu, ndi mitengo yonse: pamene iphukira, muipenya nimuzindikira pa nokha kuti dzinja lili pafupi pomwepo. Inde chotero inunso, pakuona zinthu izi zilikuchitika, zindikirani kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi. Indetu ndinena ndinu, Mbadwo uno sudzapitirira, kufikira zonse zitachitika. Kumwamba ndi dziko lapansi zidzapita; koma mau anga sadzapita. Koma mudziyang'anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha; pakuti lidzatero ndi kufikira anthu onse akukhala pankhope pa dziko lonse lapansi. Koma inu dikirani nyengo zonse, ndi kupemphera, kuti mukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzachitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wa Munthu. Ndipo usana uliwonse Iye analikuphunzitsa m'Kachisi; ndi usiku uliwonse anatuluka, nagona pa phiri lotchedwa la Azitona. Ndipo anthu onse analawira mamawa kudza kwa Iye ku Kachisi kudzamvera Iye. Ndipo phwando la mikate yopanda chotupitsa linayandikira, ndilo lotchedwa Paska. Ndipo ansembe aakulu ndi alembi anafunafuna maphedwe ake pakuti anaopa anthuwo. Ndipo Satana analowa mwa Yudasi wonenedwa Iskariote, amene anawerengedwa mmodzi wa khumi ndi awiriwo. Ndipo iye anachoka, nalankhulana ndi ansembe aakulu ndi akazembe mompereka Iye kwa iwo. Ndipo anakondwera, napangana naye kumpatsa ndalama. Ndipo iye anavomera, nafunafuna nthawi yabwino yakumpereka Iye kwa iwo, pakalibe khamu la anthu. Ndipo tsiku la mikate yopanda chotupitsa linafika, limene inayenera kuphedwa nsembe ya Paska. Ndipo Iye anatumiza Petro ndi Yohane, nati, Pitani mutikonzere ife Paska, kuti tidye. Ndipo iwo ananena naye, Mufuna tikakonzere kuti? Ndipo Iye anati kwa iwo, Onani, mutalowa m'mudzi, adzakomana ndinu munthu alikusenza mtsuko wa madzi; mumtsate ameneyo kunyumba kumene akalowako iye. Ndipo mukanene kwa mwini nyumbayo, Mphunzitsi anena nawe, Chipinda cha alendo chili kuti, m'mene ndikadye Paska pamodzi ndi ophunzira anga? Ndipo iyeyo adzakuonetsani chipinda chachikulu chapamwamba, chokonzeka; mukakonzere kumeneko. Ndipo anapita iwo, napeza monga adatero nao; ndipo anakonza Paska. Ndipo itadza nthawi yake, Iye anakhala pachakudya, ndi ophunzira pamodzi ndi Iye. Ndipo anati kwa iwo, Ndinalakalaka ndithu kudya Paska uwu pamodzi ndinu, ndisanayambe kusautsidwa; pakuti ndinena ndi inu, sindidzadya kufikira udzakwaniridwa mu Ufumu wa Mulungu. Ndipo analandira chikho, ndipo pamene adayamika, anati, Landirani ichi, muchigawane mwa inu nokha; pakuti ndinena kwa inu, kuyambira tsopano Ine sindidzamwako chipatso cha mpesa, kufikira Ufumu wa Mulungu udzafika. Ndipo m'mene adatenga mkate, nayamika, anaunyema, nawapatsa, nanena, Ichi ndi thupi langa lopatsidwa chifukwa cha inu; chitani ichi chikumbukiro changa. Ndipo choteronso chikho, atatha mgonero, nanena, Chikho ichi ndi pangano latsopano m'mwazi wanga wothiridwa chifukwa cha inu. Koma onani, dzanja lake la iye amene adzandipereka ali pagome pano pamodzi ndi Ine. Pakuti Mwana wa Munthu amukatu, monga kunaikidwiratu; koma tsoka munthuyo amene ampereka! Ndipo anayamba kufunsana mwa iwo okha, ndiye yani mwa iwo amene adzachita ichi. Ndipo kunakhala kutsutsana mwa iwo, ndani wa iwo ayesedwe wamkulu. Ndipo anati kwa iwo, Mafumu a anthu a mitundu awachitira ufumu; ndipo iwo amene awachitira ulamuliro anenedwa, Ochitira zabwino. Koma sipadzatero ndi inu; komatu iye ali wamkulu mwa inu, akhale ngati wamng'ono; ndi iye ali woyamba, akhale ngati wotumikira. Pakuti wamkulu ndani, iye wakuseama pachakudya kapena wakutumikirapo? Si ndiye wakuseama pachakudya kodi? Koma Ine ndili pakati pa inu monga ngati wotumikira. Koma inu ndinu amene munakhala ndi Ine chikhalire m'mayesero anga; ndipo Ine ndikuikirani ufumu, monganso Atate wanga anandiikira Ine, kuti mukadye ndi kumwa kugome kwanga mu Ufumu wanga; ndipo mudzakhala pa mipando yachifumu ndi kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israele. Simoni, Simoni, taona, Satana anafunsa akutengeni kuti akupeteni ngati tirigu; koma ndinakupempherera kuti chikhulupiriro chako chingazime; ndipo iwe, pamene watembenuka ukhazikitse abale ako. Ndipo anati kwa Iye, Ambuye, ndilipo ndikapite ndi Inu kundende ndi kuimfa. Ndipo Iye anati, Ndikuuza iwe, Petro, sadzalira tambala lero lino kufikira udzakana katatu kuti sundidziwa Ine. Ndipo anati kwa iwo, Pamene ndinakutumizani opanda thumba la ndalama, ndi thumba la kamba, ndi nsapato, munasowa kanthu kodi? Anati iwo, Iai. Ndipo anati kwa iwo, Koma tsopano, iye amene ali ndi thumba la ndalama, alitenge, ndi thumba la kamba lomwe; ndipo amene alibe, agulitse chofunda chake, nagule lupanga. Pakuti ndinena ndi inu, chimene chidalembedwa chiyenera kukwanitsidwa mwa Ine, Ndipo anawerengedwa ndi anthu opanda lamulo; pakuti izi za kwa Ine zili nacho chimaliziro. Ndipo iwo anati, Ambuye, taonani, malupanga awiri siwa. Ndipo anati kwa iwo, Chakwanira. Ndipo Iye anatuluka, napita monga ankachitira, kuphiri la Azitona; ndi ophunzira anamtsata Iye. Ndipo pofika pomwepo, anati kwa iwo, Pempherani kuti mungalowe m'kuyesedwa. Ndipo anapatukana nao kutalika kwake ngati kuponya mwala, nagwada pansi napemphera, nati, Atate, mukafuna Inu, chotsani chikho ichi pa Ine; koma si kufuna kwanga ai, komatu kwanu kuchitike. Ndipo anamuonekera Iye mngelo wa Kumwamba namlimbitsa Iye. Ndipo pokhala Iye m'chipsinjo mtima anapemphera kolimba koposa ndithu: ndi thukuta lake linakhala ngati madontho akulu a mwazi alinkugwa pansi. Ndipo pamene ananyamuka pakupemphera anadza kwa ophunzira, nawapeza ali m'tulo ndi chisoni, ndipo anati kwa iwo, Mugoneranji? Ukani, pempherani kuti mungalowe m'kuyesedwa. Pamene Iye anali chilankhulire, taonani, khamu la anthu, ndipo iye wotchedwa Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anawatsogolera; nayandikira Yesu kumpsompsona Iye. Koma Yesu anati kwa iye, Yudasi, ulikupereka Mwana wa Munthu ndi chimpsompsono kodi? Ndipo m'mene iwo akumzinga Iye anaona chimene chiti chichitike, anati, Ambuye, tidzakantha ndi lupanga kodi? Ndipo wina wa iwo anakantha kapolo wa mkulu wa ansembe, namdula khutu lake lamanja. Koma Yesu anayankha nati, Lolani kufikira kumene. Ndipo anakhudza khutu lake, namchiritsa. Ndipo Yesu anati kwa ansembe aakulu ndi akapitao a Kachisi, ndi akulu, amene anadza kumgwira Iye, Munatuluka ndi malupanga ndi mikunkhu kodi monga ngati kugwira wachifwamba? Masiku onse, pamene ndinali ndi inu m'Kachisi, simunatansa manja anu kundigwira: koma nyengo yino ndi yanu, ndipo ulamuliro wa mdima ndi wanu. Ndipo pamenepo anamgwira Iye, napita naye, nalowa m'nyumba ya mkulu wa ansembe. Koma Petro anatsata kutali. Ndipo pamene adasonkha moto m'kati mwa bwalo, nakhala pansi pamodzi, Petro anakhala pakati pao. Ndipo mdzakazi anamuona iye alikukhala m'kuwala kwake kwa moto, nampenyetsa iye, nati, Munthu uyunso anali naye. Koma anakana, nati, Mkaziwe, sindimdziwa Iye. Ndipo popita kamphindi, anamuona wina, nati, Iwenso uli mmodzi wa awo. Koma Petro anati, Munthu iwe, sindine. Ndipo patapita ngati ora limodzi, wina ananenetsa, kuti, Zoonadi, munthu uyunso anali naye, pakuti ndiye Mgalileya Koma Petro anati, Munthu iwe, sindidziwa chimene uchinena. Ndipo pomwepo, iye ali chilankhulire, tambala analira. Ndipo Ambuye anapotoloka, nayang'ana Petro. Ndipo Petro anakumbukira mau a Ambuye, kuti anati kwa iye, Asanalire tambala lero lino, udzandikana Ine katatu. Ndipo anatuluka, nalira misozi ndi kuwawa mtima. Ndipo amuna amene analikusunga Yesu anamnyoza Iye, nampanda. Ndipo anamkulunga Iye m'maso, namfunsa, nati, Talota; anakupanda Iwe ndani? Ndipo zambiri zina anamnenera Iye, namchitira mwano. Ndipo pamene kunacha, bungwe la akulu a anthu linasonkhana, ndiwo ansembe aakulu ndi alembi; ndipo anapita naye kubwalo lao, nanena, Ngati uli Khristu, utiuze. Ndipo anati kwa iwo, Ndikakuuzani, simudzavomereza; ndipo ndikakufunsani kanthu, simudzayankha. Koma kuyambira tsopano Mwana wa Munthu adzakhala pa dzanja lamanja la mphamvu ya Mulungu. Ndipo onse anati, Umo mtero, muli Mwana wa Mulungu kodi? Ndipo Iye anati kwa iwo, Munena kuti ndine. Ndipo iwo anati, Tifuniranjinso mboni? Pakuti ife tokha tinamva m'kamwa mwa Iye mwini. Ndipo khamu lonselo linanyamuka kupita naye kwa Pilato. Ndipo anayamba kumnenera Iye, kuti, Tinapeza munthu uyu alikupandutsa anthu a mtundu wathu, ndi kuwaletsa kupereka msonkho kwa Kaisara, nadzinenera kuti Iye yekha ndiye Khristu mfumu. Ndipo Pilato anamfunsa Iye, nanena, Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo Iye anamyankha nati, Mwatero. Ndipo Pilato anati kwa ansembe aakulu ndi makamu a anthu, Ndilibe kupeza chifukwa cha mlandu ndi munthu uyu. Koma iwo anapunda kunena kuti, Amautsa anthuwo, naphunzitsa m'Yudeya lonse, kuyambira ku Galileya ndi kufikira kuno komwe. Koma pamene Pilato anamva, anafunsa ngati munthuyu ali Mgalileya. Ndipo m'mene anadziwa kuti ali wa m'ulamuliro wake wa Herode, anamtumiza Iye kwa Herode, amene anali iye mwini ku Yerusalemu masiku awa. Ndipo Herode, pamene anaona Yesu, anakondwa ndithu; pakuti anayamba kale kufuna kumpenya Iye, chifukwa anamva za Iye; nayembekeza kuona chizindikiro china chochitidwa ndi Iye. Ndipo anamfunsa Iye mau ambiri; koma Iye sanamyankhe kanthu. Ndipo ansembe aakulu ndi alembi anaimirira, namnenera Iye kolimba. Ndipo Herode ndi asilikali ake anampeputsa Iye, namnyoza, namveka Iye chofunda chonyezimira, nambwezera kwa Pilato. Ndipo Herode ndi Pilato anachitana chibwenzi tsiku lomwelo; pakuti kale anadana. Ndipo Pilato anaitana ansembe aakulu, ndi akulu, ndi anthu, asonkhane, nati kwa iwo, Munadza kwa ine ndi munthu uyu ngati munthu wakupandutsa anthu: ndipo taonani, Ine ndinamfunsa za mlanduwu pamaso panu, ndipo sindinapeza pa munthuyu chifukwa cha zinthu zimene mumnenera; inde, ngakhale Herode yemwe; pakuti iye anambwezera Iye kwa ife; ndipo taonani, sanachite Iye kanthu kakuyenera kufa. Chifukwa chake ndidzamkwapula ndi kummasula Iye. *** Koma iwo onse pamodzi anafuula, nati, Chotsani munthu uyu, mutimasulire Barabasi; ndiye munthu anaponyedwa m'ndende chifukwa cha mpanduko m'mudzi ndi cha kupha munthu. Ndipo Pilato analankhulanso nao, nafuna kumasula Yesu; koma iwo anafuula, nanena, Mpachikeni, mpachikeni pamtanda. Ndipo anati kwa iwo nthawi yachitatu, Nanga munthuyu anachita choipa chiyani? Sindinapeza chifukwa cha kufera Iye; chotero ndidzamkwapula Iye ndi kummasula. Koma anakakamiza ndi mau okweza, napempha kuti Iye apachikidwe. Ndipo mau ao analakika. Ndipo Pilato anaweruza kuti chimene alikufunsa chichitidwe. Ndipo anawamasulira amene adaponyedwa m'ndende chifukwa cha mpanduko ndi kupha munthu, amene iwo anampempha; koma anapereka Yesu mwa chifuniro chao. Ndipo popita naye, anagwira munthu, Simoni wa ku Kirene, alikuchokera kuminda, namsenza iye mtanda aunyamule pambuyo pake pa Yesu. Ndipo unamtsata unyinji waukulu wa anthu, ndi wa akazi amene anadziguguda pachifuwa, namlirira Iye. Koma Yesu anawapotolokera nati, Ana akazi inu a Yerusalemu, musandilirire Ine, koma mudzilirire nokha ndi ana anu. Chifukwa taonani masiku alinkudza, pamene adzati, Odala ali ouma ndi mimba yosabala, ndi mawere osayamwitsa. Pomwepo adzayamba kunena kwa mapiri, Igwani pa ife; ndi kwa zitunda, Bisani ife. Pakuti ngati azichitira izi mtengo wauwisi, nanga kudzatani ndi wouma? Ndipo analinso awiri ena, ndiwo ochita zoipa, anatengedwa pamodzi ndi Iye kuti aphedwe. Ndipo pamene anafika kumalo dzina lake Bade, anampachika Iye pamtanda pomwepo, ndi ochita zoipa omwe, mmodzi kudzanja lamanja ndi wina kulamanzere. Ndipo Yesu ananena, Atate, muwakhululukire iwo, pakuti sadziwa chimene achita. Ndipo anagawana zovala zake, poyesa maere. Ndipo anthu anaima alikupenya. Ndi akulunso anamlalatira Iye, nanena, Anapulumutsa ena; adzipulumutse yekha ngati iye ndiye Khristu wa Mulungu, wosankhidwa wake. Ndipo asilikalinso anamnyoza, nadza kwa Iye, nampatsa vinyo wosasa, nanena, Ngati Iwe ndiwe mfumu ya Ayuda, udzipulumutse wekha. Ndipo kunalinso lembo pamwamba pake, ndilo: UYU NDIYE MFUMU YA AYUDA. Ndipo mmodzi wa ochita zoipa anapachikidwawo anamchitira Iye mwano nanena, Kodi suli Khristu Iwe? Udzipulumutse wekha ndi ife. Koma winayo anayankha, namdzudzula iye, nati, Kodi suopa Mulungu, poona uli m'kulangika komweku? Ndipo ifetu kuyenera; pakuti tilikulandira zoyenera zimene tinazichita: koma munthu uyu sanachite kanthu kolakwa. Ndipo ananena, Yesu, ndikumbukireni m'mene mulowa Ufumu wanu. Ndipo Iye ananena naye, Indetu, ndinena ndi iwe, Lero lino udzakhala ndine m'Paradaiso. Ndipo ora lake pamenepo linali ngati lachisanu ndi chimodzi. Ndipo panali mdima pa dziko lonse kufikira ora lachisanu ndi chinai, ndipo dzuwa linada. Ndipo nsalu yotchinga ya m'Kachisi inang'ambika pakati. Ndipo pamene Yesu anafuula ndi mau akulu, anati, Atate, m'manja mwanu ndipereka mzimu wanga. Ndipo pakutero anapereka mzimu wake. Ndipo pamene kenturiyo anaona chinachitikacho, analemekeza Mulungu, nanena, Zoonadi munthu uyu anali wolungama. Ndipo makamu onse osonkhana kudzapenya ichi, pamene anaona zinachitikazo, anapita kwao ndi kudziguguda pachifuwa. Ndipo omdziwa Iye onse, ndi akazi amene adamtsata kuchokera ku Galileya, anaima kutali, naona zinthu izi. Ndipo taonani, munthu dzina lake Yosefe, ndiye mkulu wa milandu, munthu wabwino ndi wolungama (amene sanavomereze kuweruza kwao ndi ntchito yao) wa ku Arimatea, mudzi wa Ayuda, ndiye woyembekezera Ufumu wa Mulungu, yemweyo anapita kwa Pilato napempha mtembo wake wa Yesu. Ndipo anautsitsa, naukulunga m'nsalu yabafuta, nauika m'manda osemedwa m'mwala, m'menemo sanaike munthu ndi kale lonse. Ndipo panali tsiku lokonzera, ndi Sabata linayandikira. Ndipo akazi, amene anachokera naye ku Galileya, anatsata m'mbuyo, naona manda, ndi maikidwe a mtembo wake. Ndipo anapita kwao, nakonza zonunkhira ndi mafuta abwino. Ndipo pa Sabata anapumula monga mwa lamulo. Koma tsiku loyamba la sabata, mbandakucha, anadza kumanda atatenga zonunkhira adazikonza. Ndipo anapeza mwala unakunkhunizidwa kuuchotsa pamanda. Ndipo m'mene analowa sanapeze mtembo wa Ambuye Yesu. Ndipo kunali, m'mene anathedwa nzeru nacho, taonani amuna awiri anaimirira pafupi pao atavala zonyezimira; ndipo m'mene anakhala ndi mantha naweramira pansi nkhope zao, anati kwa iwo, Mufuniranji wamoyo pa akufa? Palibe kuno Iye, komatu anauka; kumbukirani muja adalankhula nanu, pamene analinso m'Galileya, ndi kunena, kuti, Mwana wa Munthu ayenera kuperekedwa m'manja a anthu ochimwa, ndi kupachikidwa pamtanda, ndi kuuka tsiku lachitatu. Ndipo anakumbukira mau ake, nabwera kuchokera kumanda, nafotokozera zonse khumi ndi mmodziwo, ndi otsala onse omwe. Koma panali Maria wa Magadala, ndi Yohana, ndi Maria amake wa Yakobo, ndi akazi ena pamodzi nao amene ananena izi kwa atumwiwo. Ndipo mau awa anaoneka pamaso pao ngati nkhani zachabe, ndipo sanamvere akaziwo. Koma Petro ananyamuka nathamangira kumanda, ndipo powerama anaona nsalu zoyera pa zokha; ndipo anachoka nanka kwao, nazizwa ndi chija chidachitikacho. Ndipo taonani, awiri a mwa iwo analikupita tsiku lomwelo kumudzi dzina lake Emausi, wosiyana ndi Yerusalemu mastadiya makumi asanu ndi limodzi. Ndipo iwowa anakambirana nkhani za izi zonse zidachitika. Ndipo kunali m'kukambirana kwao ndi kufunsana, Yesu mwini anayandikira, natsagana nao. Koma maso ao anagwidwa kuti asamzindikire Iye. Ndipo anati kwa iwo, Mau awa ndi otani mulandizanawo poyendayenda? Ndipo anaima ndi nkhope zao zachisoni. Ndipo mmodzi wa iwo, dzina lake Kleopa, anayankha nati kwa Iye, Kodi iwe wekha ndiwe mlendo m'Yerusalemu ndi wosazindikira zidachitikazi masiku omwe ano? Ndipo anati kwa iwo, Zinthu zanji? Ndipo anati kwa Iye, Izi za Yesu Mnazarene, ndiye munthu mneneri wamphamvu m'ntchito, ndi m'mau, pamaso pa Mulungu ndi anthu onse; ndi kuti ansembe aakulu ndi akulu athu anampereka Iye ku chiweruziro cha imfa, nampachika Iye pamtanda. Ndipo tinayembekeza ife kuti Iye ndiye wakudzayo kudzaombola Israele. Komatunso, pamodzi ndi izi zonse lero ndilo tsiku lachitatu kuyambira zidachitika izi. Komatu akazi enanso a mwa ife anatidabwitsa, ndiwo amene analawirira kumanda; ndipo m'mene sanapeze mtembo wake, anadza, nanena kuti adaona m'masomphenya angelo, amene ananena kuti ali ndi moyo Iye. Ndipo ena a iwo anali nafe anachoka kunka kumanda, napeza monga momwe akazi adanena; koma Iyeyo sanamuone. Ndipo Iye anati kwa iwo, Opusa inu, ndi ozengereza mtima kusakhulupirira zonse adazilankhula aneneri! Kodi sanayenera Khristu kumva zowawa izi, ndi kulowa ulemerero wake? Ndipo anayamba kwa Mose, ndi kwa aneneri onse nawatanthauzira iwo m'malembo onse zinthu za Iye yekha. Ndipo anayandikira kumudzi umene analikupitako; ndipo anachita ngati anafuna kupitirira. Ndipo anamuumiriza Iye, nati, Khalani ndi ife; pakuti kuli madzulo, ndipo dzuwa lapendekatu. Ndipo analowa kukhala nao. Ndipo kunali m'mene Iye anaseama nao pachakudya, anatenga mkate, naudalitsa, naunyema, napatsa iwo. Ndipo maso ao anatseguka, ndipo anamzindikira Iye; ndipo anawakanganukira Iye, nawachokera. Ndipo anati wina kwa mnzake, Mtima wathu sunali wotentha m'kati mwathu nanga m'mene analankhula nafe m'njira, m'mene anatitsegulira malembo? Ndipo ananyamuka nthawi yomweyo nabwera ku Yerusalemu, napeza khumi ndi mmodziwo, ndi iwo anali nao atasonkhana pamodzi, nanena, Ambuye anauka ndithu, naonekera kwa Simoni. Ndipo iwo anawafotokozera za m'njira, ndi umo anadziwika nao m'kunyema kwa mkate. Ndipo pakulankhula izi iwowa, Iye anaimirira pakati pao; nanena nao, Mtendere ukhale nanu. Koma anaopsedwa ndi kuchita mantha, nayesa alikuona mzimu. Ndipo anati kwa iwo, Mukhala bwanji ovutika? Ndipo matsutsano amauka bwanji m'mtima mwanu? Penyani manja anga ndi mapazi anga, kuti Ine ndine mwini: ndikhudzeni, ndipo penyani; pakuti mzimu ulibe mnofu ndi mafupa, monga muona ndili nazo Ine. Ndipo m'mene ananena ichi, anawaonetsera iwo manja ake ndi mapazi ake. Koma pokhala iwo chikhalire osakhulupirira chifukwa cha chimwemwe, nalikuzizwa, anati kwa iwo, Muli nako kanthu kakudya kuno? Ndipo anampatsa Iye chidutsu cha nsomba yokazinga. Ndipo anachitenga, nachidya pamaso pao. Ndipo anati kwa iwo, Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi Masalmo. Ndipo anawatsegulira mitima yao, kuti adziwitse malembo; ndipo anati kwa iwo, Kotero kwalembedwa, kuti Khristu amve zowawa, nauke kwa akufa tsiku lachitatu; ndi kuti kulalikidwe m'dzina lake kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo kwa mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu. Inu ndinu mboni za izi. Ndipo onani, Ine nditumiza pa inu lonjezano la Atate wanga; koma khalani inu m'mudzi muno, kufikira mwavekedwa ndi mphamvu yochokera Kumwamba. Ndipo anatuluka nao kufikira ku Betaniya; nakweza manja ake, nawadalitsa. Ndipo kunali, pakuwadalitsa Iye analekana nao, natengedwa kunka Kumwamba. Ndipo anamlambira Iye, nabwera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu; ndipo anakhala chikhalire m'Kachisi, nalikuyamika Mulungu. Amen. Pachiyambi panali Mau, ndipo Mau anali kwa Mulungu, ndipo Mau ndiye Mulungu. Awa anali pachiyambi kwa Mulungu. Zonse zinalengedwa ndi Iye; ndipo kopanda Iye sikunalengedwa kanthu kalikonse kolengedwa. Mwa Iye munali moyo; ndi moyowu unali kuunika kwa anthu. Ndipo kuunikaku kunawala mumdima; ndi mdimawu sunakuzindikira. Kunali munthu, wotumidwa ndi Mulungu, dzina lake ndiye Yohane. Iyeyu anadza mwa umboni kudzachita umboni za kuunikaku, kuti onse akakhulupirire mwa iye. Iye sindiye kuunikaku, koma anatumidwa kukachita umboni wa kuunikaku. Uku ndiko kuunika kwenikweni, kumene kuunikira anthu onse akulowa m'dziko lapansi. Anali m'dziko lapansi, ndi dziko linalengedwa ndi Iye, koma dziko silinamzindikira Iye. Anadza kwa zake za Iye yekha, ndipo ake a mwini yekha sanamlandire Iye. Koma onse amene anamlandira Iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lake; amene sanabadwe ndi mwazi, kapena ndi chifuniro cha thupi, kapena ndi chifuniro cha munthu, koma cha Mulungu. Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi. Yohane achita umboni za Iye, nafuula nati, Uyu ndiye amene ndinanena za Iye, Wakudzayo pambuyo panga analipo ndisanabadwe ine; chifukwa anakhala woyamba wa ine. Chifukwa mwa kudzala kwake tinalandira ife tonse, chisomo chosinthana ndi chisomo. Chifukwa chilamulo chinapatsidwa mwa Mose; chisomo ndi choonadi zinadza mwa Yesu Khristu. Kulibe munthu anaona Mulungu nthawi zonse; Mwana wobadwa yekha wakukhala pa chifuwa cha Atate, Iyeyu anafotokozera. Ndipo umene ndiwo umboni wa Yohane, pamene Ayuda anatuma kwa iye ansembe ndi Alevi a ku Yerusalemu akamfunse iye, Ndiwe yani? Ndipo anavomera, wosakana; nalola kuti, Sindine Khristu. Ndipo anamfunsa iye, Nanga bwanji? Ndiwe Eliya kodi? Nanena iye, Sindine iye. Ndiwe Mneneriyo kodi? Nayankha, Iai. Chifukwa chake anati kwa iye, Ndiwe yani? Kuti tibwezere mau kwa iwo anatituma ife. Unena chiyani za iwe wekha? Anati, Ndine mau a wofuula m'chipululu, Lungamitsani njira ya Mbuye, monga anati Yesaya mneneriyo. Ndipo otumidwawo anali a kwa Afarisi. Ndipo anamfunsa iye, nati kwa iye, Koma ubatiza bwanji, ngati suli Khristu, kapena Eliya, kapena Mneneriyo? Yohane anawayankha, nati, Ine ndibatiza ndi madzi; pakati pa inu paimirira amene simumdziwa, ndiye wakudza pambuyo panga, amene sindiyenera kummasulira lamba la nsapato yake. Zinthu izi zinachitika m'Betaniya tsidya lija la Yordani, pomwe analikubatiza Yohane. M'mawa mwake anaona Yesu alinkudza kwa iye, nanena, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi! Ndiye amene ndinati za Iye, Pambuyo panga palinkudza munthu amene analipo ndisanabadwe ine; pakuti anali woyamba wa ine. Ndipo sindinamdziwa Iye; koma kuti aonetsedwe kwa Israele, chifukwa cha ichi ndinadza ine kudzabatiza ndi madzi. Ndipo Yohane anachita umboni, nati, Ndinaona Mzimu alikutsika kuchokera Kumwamba monga nkhunda; nakhalabe pa Iye. Ndipo sindinamdziwa Iye, koma wonditumayo kudzabatiza ndi madzi, Iyeyu ananena ndi ine, Amene udzaona Mzimu atsikira, nakhala pa Iye, yemweyu ndiye wakubatiza ndi Mzimu Woyera. Ndipo ndaona ine, ndipo ndachita umboni kuti Mwana wa Mulungu ndi Yemweyu. M'mawa mwakenso analikuimirira Yohane ndi awiri a ophunzira ake; ndipo poyang'ana Yesu alikuyenda, anati, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu! Ndipo ophunzira awiriwo anamva iye alinkulankhula, natsata Yesu. Koma Yesu anacheuka, napenya iwo alikumtsata, nanena nao, Mufuna chiyani? Ndipo anati kwa Iye, Rabi (ndiko kunena posandulika, Mphunzitsi), mukhala kuti? Nanena nao, Tiyeni, mukaone. Pamenepo anadza naona kumene anakhala; nakhala ndi Iye tsiku lomwelo; panali monga ora lakhumi. Andrea mbale wake wa Simoni Petro anali mmodzi wa awiriwo, anamva Yohane, namtsata Iye. Anayamba iye kupeza mbale wake yekha Simoni, nanena naye, Tapeza ife Mesiya (ndiko kusandulika Khristu). Anadza naye kwa Yesu. M'mene anamyang'ana iye, anati, Uli Simoni mwana wa Yohane; udzatchedwa Kefa (ndiko kusandulika Petro). M'mawa mwake anafuna kutuluka kunka ku Galileya, napeza Filipo. Ndipo Yesu ananena naye, Tsata Ine. Koma Filipo anali wa ku Betsaida, mudzi wa Andrea ndi Petro. Filipo anapeza Natanaele, nanena naye, Iye amene Mose analembera za Iye m'chilamulo, ndi aneneri, tampeza, ndiye Yesu mwana wa Yosefe wa ku Nazarete. Natanaele anati kwa iye, Ku Nazarete nkutha kuchokera kanthu kabwino kodi? Filipo ananena naye, Tiye ukaone. Yesu anaona Natanaele alinkudza kwa Iye, nanena za iye, Onani, Mwisraele ndithu, mwa iye mulibe chinyengo! Natanaele ananena naye, Munandidziwira kuti? Yesu anayankha nati kwa iye, Asanakuitane Filipo, pokhala iwe pansi pa mkuyu paja, ndinakuona iwe. Natanaele anayankha Iye, Rabi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu, ndinu mfumu ya Israele. Yesu anayankha nati kwa iye, Chifukwa ndinati kwa iwe kuti ndinakuona pansi pa mkuyu ukhulupirira kodi? Udzaona zoposa izi. Ndipo ananena naye, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Mudzaona thambo lotseguka, ndi angelo a Mulungu akwera natsikira pa Mwana wa Munthu. Ndipo tsiku lachitatu panali ukwati m'Kana wa m'Galileya; ndipo amake wa Yesu anali komweko. Ndipo Yesu yemwe ndi ophunzira ake anaitanidwa kuukwatiwo. Ndipo pakutha vinyo, amake wa Yesu ananena naye, Alibe vinyo. Yesu nanena naye, Mkazi, ndili ndi chiyani ndi inu? Nthawi yanga siinafike. Amake ananena kwa atumiki, Chimene chilichonse akanena kwa inu, chitani. Ndipo panali pamenepo mitsuko yamiyala isanu ndi umodzi yoikidwako monga mwa mayeretsedwe a Ayuda, yonse ya miyeso iwiri kapena itatu. Yesu ananena nao, Dzazani mitsukoyo ndi madzi. Naidzaza, ndendende. Ndipo ananena nao, Tungani tsopano, mupite nao kwa mkulu wa phwando. Ndipo anapita nao. Koma pamene mkuluyo analawa madzi osanduka vinyowo, ndipo sanadziwe kumene anachokera (koma atumiki amene adatunga madzi anadziwa), mkuluyo anaitana mkwati, nanena naye, Munthu aliyense amayamba kuika vinyo wokoma; ndipo anthu atamwatu, pamenepo wina wosakoma; koma iwe wasunga vinyo wokoma kufikira tsopano lino. Chiyambi ichi cha zizindikiro zake Yesu anachita m'Kana wa m'Galileya naonetsera ulemerero wake; ndipo ophunzira ake anakhulupirira Iye. Zitapita izi anatsikira ku Kapernao, Iye ndi amake, ndi abale ake, ndi ophunzira ake; nakhala komweko masiku owerengeka. Ndipo Paska wa Ayuda unayandikira, ndipo Yesu anakwera kunka ku Yerusalemu. Ndipo anapeza m'Kachisi iwo akugulitsa ng'ombe ndi nkhosa ndi nkhunda, ndi akusinthana ndalama alikukhala pansi. Ndipo pamene adapanga mkwapulo wazingwe, anatulutsa onse m'Kachisimo, ndi nkhosa ndi ng'ombe; nakhuthula ndalama za osinthanawo, nagubuduza magome; nati kwa iwo akugulitsa nkhunda, Chotsani izi muno; musamayesa nyumba ya Atate wanga nyumba ya malonda. Ophunzira ake anakumbukira kuti kunalembedwa, Changu cha pa nyumba yanu chandidya ine. Chifukwa chake Ayuda anayankha nati kwa Iye, Mutionetsera ife chizindikiro chanji, pakuti muchita izi? Yesu anayankha nati kwa iwo, Pasulani Kachisi uyu, ndipo masiku atatu ndidzamuutsa. Pamenepo Ayuda anati, Zaka makumi anai ndi zisanu ndi chimodzi analimkumanga Kachisiyu, kodi inu mudzamuutsa masiku atatu? Koma Iye analikunena za Kachisi wa thupi lake. Chifukwa chake atauka kwa akufa, ophunzira ake anakumbukira kuti ananena ichi; ndipo anakhulupirira cholemba, ndi mau amene Yesu ananena. Koma pamene anali m'Yerusalemu pa Paska pachikondwerero, ambiri anakhulupirira dzina lake, pakuona zizindikiro zake zimene anachitazi. Koma Yesu sanakhulupirire iwo kuti akhale nao, chifukwa Iye anadziwa anthu onse, ndipo sanasowe wina achite umboni za munthu; pakuti anadziwa Iye yekha chimene chinali mwa munthu. Koma panali munthu wa Afarisi, dzina lake Nikodemo, mkulu wa Ayuda. Iyeyu anadza kwa Yesu usiku, nati kwa Iye, Rabi, tidziwa kuti Inu ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kuchita zizindikiro zimene Inu muchita, ngati Mulungu sakhala naye. Yesu anayankha nati kwa iye, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuona Ufumu wa Mulungu. Nikodemo ananena kwa Iye, Munthu akhoza bwanji kubadwa atakalamba? Kodi akhoza kulowanso m'mimba ya amake ndi kubadwa? Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu. Chobadwa m'thupi chikhala thupi, ndipo chobadwa mwa Mzimu, chikhala mzimu. Usadabwe chifukwa ndinati kwa iwe, Uyenera kubadwa mwatsopano. Mphepo iomba pomwe ifuna, ndipo ukumva mau ake, koma sudziwa kumene ichokera, ndi kumene imuka; chotero aliyense wobadwa mwa Mzimu. Nikodemo anayankha nati kwa Iye, Izi zingatheke bwanji? Yesu anayankha nati kwa iye, Kodi uli mphunzitsi wa Israele, ndipo sudziwa izi? Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, Tilankhula chimene tichidziwa, ndipo tichita umboni za chimene tachiona; ndipo umboni wathu simuulandira. Ngati ndakuuzani za pansi pano, ndipo simukhulupirira, mudzakhulupirira bwanji, ngati ndikuuzani za Kumwamba? Ndipo kulibe munthu anakwera Kumwamba, koma Iye wotsikayo kuchokera Kumwamba, ndiye Mwana wa Munthu, wokhala m'Mwambayo. Ndipo monga Mose anakweza njoka m'chipululu, chotero Mwana wa Munthu ayenera kukwezedwa; kuti yense wakukhulupirira akhale nao moyo wosatha mwa Iye. Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha. Pakuti Mulungu sanatume Mwana wake kudziko lapansi, kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe ndi Iye. Wokhulupirira Iye saweruzidwa; wosakhulupirira waweruzidwa ngakhale tsopano, chifukwa sanakhulupirire dzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu. Koma chiweruziro ndi ichi, kuti kuunika kunadza kudziko lapansi, ndipo anthu anakonda mdima koposa kuunika; pakuti ntchito zao zinali zoipa. Pakuti yense wakuchita zoipa adana nako kuunika, ndipo sakudza kwa kuunika, kuti zingatsutsidwe ntchito zake. Koma wochita choonadi adza kukuunika, kuti ntchito zake zionekere kuti zinachitidwa mwa Mulungu. Zitapita izi anadza Yesu ndi ophunzira ake kudziko la Yudeya; ndipo pamenepo anatsotsa nao pamodzi, nabatiza. Ndipo Yohane analinkubatiza m'Ainoni pafupi pa Salimu, chifukwa panali madzi ambiri pamenepo; ndipo analinkufikako anthu, nalinkubatizidwa. Pakuti Yohane sanaikidwe m'ndende. Pamenepo padauka kufunsana mwa ophunzira ake a Yohane ndi Myuda za mayeretsedwe. Ndipo anadza kwa Yohane, nati kwa iye, Rabi, Iye amene anali ndi inu tsidya lija la Yordani, amene munamchitira umboni, taonani yemweyu abatiza, ndipo anthu onse alinkudza kwa Iye. Yohane anayankha nati, Munthu sakhoza kulandira kanthu, ngati sikapatsidwa kwa iye kuchokera Kumwamba. Inu nokha mundichitira umboni, kuti ndinati, Sindine Khristu, koma kuti ndili wotumidwa m'tsogolo mwake mwa Iye. Iye amene ali naye mkwatibwi ali mkwati, koma mnzake wa mkwatiyo, wakuimirira ndi kumvera iye, akondwera kwakukulu chifukwa cha mau a mkwatiyo; chifukwa chake chimwemwe changa chimene chakwanira. Iyeyo ayenera kukula koma ine ndichepe. Iye wochokera Kumwamba ali woposa onse; iye amene ali wa dziko lapansi ali wa dziko lapansi, nalankhula za dziko lapansi: Iye wochokera Kumwamba ali woposa onse. Chimene anachiona nachimva, achita umboni wa ichi chomwe; ndipo kulibe munthu alandira umboni wake. Iye amene analandira umboni wake anaikapo chizindikiro chake kuti Mulungu ali woona. Pakuti Iye amene Mulungu anamtuma alankhula mau a Mulungu; pakuti sapatsa Mzimu ndi muyeso. Atate akonda Mwana, nampatsa zinthu zonse m'dzanja lake. Iye amene akhulupirira Mwanayo ali nao moyo wosatha; koma iye amene sakhulupirira Mwanayo sadzaona moyo, koma mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye. Chifukwa chake pamene Ambuye anadziwa kuti Afarisi adamva kuti Yesu anayesa anthu ophunzira, nawabatiza koposa Yohane (angakhale Yesu sanabatize yekha koma ophunzira ake), anachokera ku Yudeya, namukanso ku Galileya. Ndipo anayenera kupita pakati pa Samariya. Chifukwa chake anadza kumudzi wa Samariya, dzina lake Sikari, pafupi pa kadziko kamene Yakobo adapatsa mwana wake Yosefe; ndipo pamenepo panali chitsime cha Yakobo. Ndipo Yesu, popeza analema ndi ulendo wake, motero anakhala ndi ulendo wake, motero anakhala pachitsime. Kunali ngati ora lachisanu ndi chimodzi. Kunadza mkazi wotuluka m'Samariya kudzatunga madzi. Yesu ananena naye, Undipatse Ine ndimwe. Pakuti ophunzira ake adachoka kunka kumudzi kuti akagule chakudya. Pamenepo mkazi wa m'Samariya ananena ndi Iye, Bwanji Inu, muli Myuda, mupempha kwa ine kumwa, ndine mkazi Msamariya? (Pakuti Ayuda sayenderana nao Asamariya). Yesu anayankha nati kwa iye, Ukadadziwa mtulo wa Mulungu, ndi Iye amene alinkunena ndi iwe, Undipatse Ine ndimwe; ukadapempha Iye, ndipo akadakupatsa madzi amoyo. Mkaziyo ananena ndi Iye, Ambuye, mulibe chotungira madzi, ndi chitsime chili chakuya; ndipo mwatenga kuti madzi amoyo? Kodi muli wamkulu ndi atate wathu Yakobo amene anatipatsa ife chitsimechi, namwamo iye yekha, ndi ana ake, ndi zoweta zake? Yesu anayankha nati kwa iye, Yense wakumwako madzi awa adzamvanso ludzu; koma iye wakumwa madzi amene Ine ndidzampatsa sadzamva ludzu nthawi zonse; koma madzi amene Ine ndidzampatsa adzakhala mwa iye kasupe wa madzi otumphukira kumoyo wosatha. Mkaziyo ananena kwa Iye, Ambuye, ndipatseni madzi amene, kuti ndisamve ludzu, kapena ndisadze kuno kudzatunga. Yesu ananena kwa iye, Muka, kamuitane mwamuna wako, nudze kuno. Mkazi anayankha nati kwa Iye, Ndilibe mwamuna. Yesu ananena naye, Wanena bwino, kuti mwamuna ndilibe; pakuti wakhala nao amuna asanu; ndipo iye amene ukhala naye tsopano sali mwamuna wako; ichi wanena zoona. Mkazi ananena ndi Iye, Ambuye, ndizindikira kuti muli Mneneri. Makolo athu analambira m'phiri ili; ndipo inu munena, kuti m'Yerusalemu muli malo oyenera kulambiramo anthu. Yesu ananena naye, Tamvera Ine, mkazi iwe, kuti ikudza nthawi, imene simudzalambira Atate kapena m'phiri ili, kapena m'Yerusalemu. Inu mulambira chimene simuchidziwa; ife tilambira chimene tichidziwa; pakuti chipulumutso chichokera kwa Ayuda. Koma ikudza nthawi, ndipo tsopano ilipo, imene olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m'choonadi; pakuti Atate afuna otere akhale olambira ake. Mulungu ndiye mzimu; ndipo omlambira Iye ayenera kumlambira mumzimu ndi m'choonadi. Mkazi ananena ndi Iye, Ndidziwa kuti Mesiya adza (wotchedwa Khristu): akadzadza Iyeyu, adzatiuza zonse. Yesu ananena naye, Ine wakulankhula nawe ndine amene. Ndipo pamenepo anadza ophunzira ake; nazizwa kuti analinkulankhula ndi mkazi; koma panalibe wina anati, Mufuna chiyani? Kapena, mulankhula naye chiyani? Pamenepo mkazi anasiya mtsuko wake, namuka kumudzi, nanena ndi anthu, Tiyeni, mukaone munthu, amene anandiuza zinthu zilizonse ndinazichita: ameneyu sali Khristu nanga? Anatuluka iwo m'mudzi ndipo analinkudza kwa Iye. Pa mphindikati iyi ophunzira ake anampempha Iye, ndi kunena, Rabi, idyani. Koma Iye anati kwa iwo, Ine ndili nacho chakudya chimene inu simuchidziwa. Chifukwa chake ophunzira ananena wina ndi mnzake, Kodi pali wina anamtengera Iye kanthu kakudya? Yesu ananena nao, Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza ntchito yake. Kodi simunena inu, kuti, Yatsala miyezi inai, ndipo kudza kumweta? Onani ndinena kwa inu, Kwezani maso anu, nimuyang'ane m'minda, kuti mwayera kale kufikira kumweta. Wakumweta alandira kulipira, nasonkhanitsira chobala kumoyo wosatha; kuti wofesayo akakondwere pamodzi ndi womwetayo. Pakuti m'menemo chonenacho chili choona, Wofesa ndi wina, womweta ndi winanso. Ine ndinatuma inu kukamweta chimene simunagwirirapo ntchito: ena anagwira ntchito, ndipo inu mwalowa ntchito yao. Ndipo m'mudzi muja anthu Asamariya ambiri anamkhulupirira Iye chifukwa cha mau a mkazi, wochita umboniyo, kuti, Anandiuza ine zinthu zilizonse ndinazichita. Chifukwa chake pamene Asamariya anadza kwa Iye, anamfunsa akhale nao; ndipo anakhala komweko masiku awiri. Ndipo ambiri oposa anakhulupirira chifukwa cha mau ake; ndipo ananena kwa mkazi, kuti, Tsopano sitikhulupirira chifukwa cha kulankhula kwako: pakuti tamva tokha, ndipo tidziwa kuti Mpulumutsi wa dziko lapansi ndi Iyeyu ndithu. Koma atapita masiku awiriwo anachoka komweko kunka ku Galileya. Pakuti Yesu mwini anachita umboni kuti, Mneneri alibe ulemu m'dziko la kwao. Chifukwa chake pamene anadza ku Galileya, Agalileya anamlandira Iye, atakaona zonse zimene anazichita m'Yerusalemu pachikondwerero; pakuti iwonso ananka kuchikondwerero. Chifukwa chake Yesu anadzanso ku Kana wa m'Galileya, kumene anasandutsa madzi vinyo. Ndipo kunali mkulu wina wa mfumu, mwana wake anadwala m'Kapernao. Iyeyu, pamene anamva kuti Yesu wachokera ku Yudeya nafika ku Galileya, ananka kwa Iye, nampempha kuti atsike kukachiritsa mwana wake; pakuti anali pafupi imfa. Pamenepo Yesu anati kwa iye, Ngati simuona zizindikiro ndi zozizwa, simudzakhulupirira. Mkuluyo ananena kwa Iye, Ambuye, tsikani asanafe mwana wanga. Yesu ananena naye, Muka, mwana wako ali ndi moyo. Munthuyo anakhulupirira mau amene Yesu anatero naye, namuka. Ndipo m'mene analikutsika, akapolo ake anakomana naye, nanena, kuti, Mwana wanu ali ndi moyo. Chifukwa chake anawafunsa ora lake anayamba kuchiralo. Pamenepo anati kwa iye, kuti, Dzulo, ora lachisanu ndi chiwiri malungo anamsiya. Chifukwa chake atateyo anadziwa kuti ndi ora lomwelo limene Yesu anati kwa iye, Mwana wako ali ndi moyo; ndipo anakhulupirira iye yekha ndi a pa banja lake onse. Ichi ndi chizindikiro chachiwiri Yesu anachita, atachokera ku Yudeya, ndi kulowa m'Galileya. Zitapita izi panali chikondwerero cha Ayuda; ndipo Yesu anakwera kunka ku Yerusalemu. Koma pali thamanda m'Yerusalemu pa Chipata cha Nkhosa, lotchedwa m'Chihebri Betesida, lili ndi makonde asanu. M'menemo munagona khamu lalikulu la anthu odwala, akhungu, opunduka miyendo, opuwala. *** Koma panali munthu wina apo, ali m'kudwala kwake zaka makumi atatu kudza zisanu ndi zitatu. Yesu, pakuona ameneyo alikugona, ndipo anadziwa kuti anatero nthawi yaikulu pamenepo, ananena naye, Ufuna kuchiritsidwa kodi? Wodwalayo anayankha, Ambuye, ndilibe wondiviika ine m'thamanda, paliponse madzi avundulidwa; koma m'mene ndilinkudza ine, wina atsika ndisanatsike ine. Yesu ananena naye, Tauka, yalula mphasa yako, nuyende. Ndipo pomwepo munthuyu anachira, nayalula mphasa yake, nayenda. Koma tsiku lomwelo linali la Sabata. Chifukwa chake Ayuda ananena kwa wochiritsidwayo, Ndi Sabata, ndipo sikuloledwa kwa iwe kuyalula mphasa yako. Koma iyeyu anayankha iwo, Iye amene anandichiritsa, yemweyu anati kwa ine, Yalula mphasa yako, nuyende. Anamfunsa, Munthuyo ndani wonena ndi iwe, Yalula mphasa yako, nuyende? Koma wochiritsidwayo sanadziwe kuti anali ndani; pakuti Yesu anachoka kachetechete, popeza panali anthu aunyinji m'malo muja. Zitapita izi Yesu anampeza m'Kachisi, nati kwa iye, Taona, wachiritsidwa; usachimwenso, kuti chingakugwere choipa choposa. Munthuyo anachoka, nauza Ayuda, kuti ndiye Yesu amene adamchiritsa. Ndipo chifukwa cha ichi Ayuda analondalonda Yesu, popeza anachita izo tsiku la Sabata. Koma Yesu anayankha iwo, Atate wanga amagwira ntchito kufikira tsopano, Inenso ndigwira ntchito. Chifukwa cha ichi Ayuda anaonjeza kufuna kumupha, si chifukwa cha kuswa tsiku la Sabata kokha, komatu amatchanso Mulungu Atate wake wa Iye yekha; nadziyesera wolingana ndi Mulungu. Pamenepo Yesu anayankha nati kwa iwo, Indetu, indetu ndinena kwa inu, sakhoza Mwana kuchita kanthu pa yekha, koma chimene aona Atate achichita, ndicho. Pakuti zimene Iye azichita, zomwezo Mwananso azichita momwemo. Pakuti Atate akonda Mwana, namuonetsa zonse azichita yekha: ndipo adzamuonetsa ntchito zoposa izi, kuti mukazizwe. Pakuti monga Atate aukitsa akufa, nawapatsa moyo, momwemonso Mwana apatsa moyo iwo amene Iye afuna. Pakuti Atate saweruza munthu aliyense, koma anapereka kuweruza konse kwa Mwana; kuti onse akalemekeze Mwana, monga alemekeza Atate. Wosalemekeza Mwana salemekeza Atate amene anamtuma Iye. Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti iye wakumva mau anga, ndi kukhulupirira Iye amene anandituma Ine, ali nao moyo wosatha, ndipo salowa m'kuweruza, koma wachokera kuimfa, nalowa m'moyo. Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti ikudza nthawi, ndipo ilipo tsopano, imene akufa adzamva mau a Mulungu; ndipo iwo akumva adzakhala ndi moyo. Pakuti monga Atate ali ndi moyo mwa Iye yekha, momwemonso anapatsa kwa Mwana kukhala ndi moyo mwa Iye yekha; ndipo anampatsa Iye mphamvu ya kuchita mlandu, pakuti ali Mwana wa Munthu. Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthawi, imene onse ali m'manda adzamva mau ake, nadzatulukira, amene adachita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adachita zoipa kukuuka kwa kuweruza. Sindikhoza kuchita kanthu kwa Ine ndekha; monga momwe ndimva ndiweruza; ndipo maweruzidwe anga ali olungama; chifukwa kuti sinditsata chifuniro changa, koma chifuniro cha Iye wondituma Ine. Ngati ndichita umboni wa Ine ndekha, umboni wanga suli woona. Wochita umboni wa Ine ndi wina; ndipo ndidziwa kuti umboni umene Iye andichitire Ine uli woona. Inu munatuma kwa Yohane, ndipo iye anachitira umboni choonadi. Ndipo Ine sindilandira umboni kwa munthu: koma ndinena izi, kuti inu mukapulumutsidwe. Iyeyo anali nyali yoyaka ndi yowala; ndipo inu munafuna kukondwera m'kuunika kwake kanthawi. Koma Ine ndili nao umboni woposa wa Yohane; pakuti ntchito zimene Atate anandipatsa ndizitsirize, ntchito zomwezo ndizichita zindichitira umboni, kuti Atate anandituma Ine. Ndipo Atate wonditumayo, Iyeyu wandichitira Ine umboni. Simunamva mau ake konse, kapena maonekedwe ake simunaona. Ndipo mulibe mau ake okhala mwa inu; chifukwa kuti amene Iyeyu anatuma, inu simumkhulupirira ameneyo. Musanthula m'malembo, popeza muyesa kuti momwemo muli nao moyo wosatha; ndipo akundichitira Ine umboni ndi iwo omwewo; ndipo simufuna kudza kwa Ine, kuti mukhale nao moyo. Ulemu sindiulandira kwa anthu. Koma ndikudziwani inu, kuti mulibe chikondi cha Mulungu mwa inu nokha. Ndadza Ine m'dzina la Atate wanga, ndipo simundilandira Ine; akadza wina m'dzina lake la iye mwini, iyeyu mudzamlandira. Mungathe inu bwanji kukhulupirira, popeza mulandira ulemu wina kwa mnzake ndipo ulemu wakuchokera kwa Mulungu yekha simuufuna? Musayesa kuti Ine ndidzakunenezani inu kwa Atate; pali wakukunenezani, ndiye Mose, amene inu mumtama. Pakuti mukadakhulupirira Mose, mukadakhulupirira Ine; pakuti iyeyu analembera za Ine. Koma ngati simukhulupirira malembo a iyeyu, mudzakhulupirira bwanji mau anga? Zitapita izi anachoka Yesu kunka kutsidya lija la nyanja ya Galileya, ndiyo ya Tiberiasi. Ndipo khamu lalikulu la anthu linamtsata Iye, chifukwa anaona zizindikiro zimene anachita pa odwala. Koma Yesu anakwera kuphiri, nakhala pansi komweko pamodzi ndi ophunzira ake. Ndipo Paska, chikondwerero cha Ayuda, anayandikira. Pamenepo Yesu, pokweza maso ake, ndi kuona kuti khamu lalikulu lilinkudza kwa Iye, ananena kwa Filipo, Tidzagula kuti mikate kuti adye awa? Koma ananena ichi kuti amuyese; pakuti anadziwa yekha chimene adzachita. Filipo anayankha Iye, Mikate ya marupiya atheka mazana awiri siikwanira iwo, kuti yense atenge pang'ono. Mmodzi wa ophunzira ake, Andrea, mbale wake wa Simoni Petro, ananena ndi Iye, Pali mnyamata pano, amene ali nayo mikate isanu yabarele, ndi tinsomba tiwiri; koma nanga izi zifikira bwanji ambiri otere? Nati Yesu, Akhalitseni anthu pansi. Ndipo panali udzu wambiri pamalopo. Pamenepo amunawo anakhala pansi, kuwerenga kwao monga zikwi zisanu. Pomwepo Yesu anatenga mikateyo; ndipo pamene adayamika, anagawira iwo akukhala pansi; momwemonso ndi tinsomba, monga momwe iwo anafuna. Ndipo pamene adakhuta, Iye ananena kwa ophunzira ake, Sonkhanitsani makombo kuti kasatayike kanthu. Pomwepo anasonkhanitsa, nadzaza madengu khumi ndi awiri ndi makombo a mikate isanuyo yabarele, amene anatsalira anadyawo. Chifukwa chake, anthu, poona chizindikiro chimene anachita, ananena, kuti, Ameneyo ndiye mneneri ndithu wakudzayo m'dziko lapansi. Pamenepo Yesu, pozindikira kuti alikufuna kudza kudzamgwira Iye, kuti amlonge ufumu, anachokanso kunka kuphiri pa yekha. Koma pofika madzulo, ophunzira ake anatsikira kunyanja; ndipo pamene adalowa m'ngalawa, analikuoloka nyanja kunka ku Kapernao. Ndipo kutada pamenepo, koma Yesu asanadze kwa iwo. Ndipo nyanja inalikuuka chifukwa cha mphepo yaikulu yakuombako. Ndipo pamene adapalasa monga mastadiya makumi awiri ndi asanu kapena makumi atatu, anaona Yesu alikuyenda panyanja, ndi kuyandikira ngalawa; ndipo anachita mantha. Koma Iye ananena nao, Ndine; musaope. Pamenepo analola kumlandira m'ngalawa; ndipo pomwepo ngalawayo inafika kumtunda kumene analikunkako. M'mawa mwake khamu la anthu limene linaima tsidya lija la nyanja linaona kuti palibe ngalawa ina koma imodzi, ndi kuti Yesu sanalowe pamodzi ndi ophunzira ake m'ngalawamo, koma ophunzira ake adachoka pa okha; koma zinachokera ngalawa zina ku Tiberiasi, pafupi pa malo pomwe adadyapo mkate m'mene Ambuye Yesu adayamika; chifukwa chake pamene khamu la anthu linaona kuti palibe Yesu, ndi ophunzira ake palibe, iwo okha analowa m'ngalawazo nadza ku Kapernao, alikufuna Yesu. Ndipo pamene anampeza Iye tsidya lina la nyanja, anati kwa Iye, Rabi, munadza kuno liti? Yesu anayankha iwo nati, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Mundifuna Ine, si chifukwa munaona zizindikiro, koma chifukwa munadya mkate, nimunakhuta. Gwirani ntchito si chifukwa cha chakudya chimene chitsalira kumoyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani inu; pakuti ameneyo Atate, ndiye Mulungu, adamlembera chizindikiro. Pamenepo anati kwa Iye, Tichite chiyani, kuti tichite ntchito za Mulungu? Yesu anayankha nati kwa iwo, Ntchito ya Mulungu ndi iyi, kuti mukhulupirire Iye amene Iyeyo anamtuma. Chifukwa chake anati kwa Iye, Ndipo muchita chizindikiro chanji, kuti tione ndi kukhulupirira Inu? Muchita chiyani? Atate athu anadya mana m'chipululu; monga kwalembedwa, Mkate wochokera m'mwamba anawapatsa iwo kudya. Chifukwa chake Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Si Mose amene anakupatsani inu mkate wa Kumwamba; koma Atate wanga akupatsani inu mkate woona wa Kumwamba. Pakuti mkate wa Mulungu ndiye wakutsika kuchokera Kumwamba ndi kupatsa moyo kwa dziko lapansi. Pamenepo anati kwa Iye, Ambuye, tipatseni ife mkate umene nthawi zonse. Yesu anati kwa iwo, Ine ndine mkate wamoyo; iye amene adza kwa Ine sadzamva njala, ndi iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu nthawi zonse. Koma ndinati kwa inu, kuti mungakhale mwandiona, simukhulupirira. Chinthu chonse chimene anandipatsa Ine Atate chidzadza kwa Ine; ndipo wakudza kwa Ine sindidzamtaya iye kunja. Pakuti ndinatsika Kumwamba, si kuti ndichite chifuniro changa, koma chifuniro cha Iye amene anandituma Ine. Koma chifuniro cha Iye amene anandituma Ine ndi ichi, kuti za ichi chonse Iye anandipatsa Ine ndisatayeko kanthu, koma ndichiukitse tsiku lomaliza. Pakuti chifuniro cha Atate wanga ndi ichi, kuti yense wakuyang'ana Mwana, ndi kukhulupirira Iye, akhale nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza. Chifukwa chake Ayuda anang'ung'udza za Iye, chifukwa anati, Ine ndine mkate wotsika Kumwamba. Ndipo iwo ananena, Si Yesu uyu, mwana wa Yosefe, atate wake ndi amai wake tiwadziwa? Anena bwanji tsopano, kuti, Ndinatsika Kumwamba? Yesu anayankha nati kwa iwo, Musang'ung'udze wina ndi mnzake. Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine amkoka iye; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza. Chalembedwa mwa aneneri, Ndipo adzakhala onse ophunzitsidwa ndi Mulungu. Yense amene adamva kwa Atate, naphunzira, adza kwa Ine. Sikuti munthu wina waona Atate, koma Iye amene ali wochokera kwa Mulungu, ameneyo waona Atate. Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wokhulupirira ali nao moyo wosatha. Ine ndine mkate wamoyo. Makolo anu adadya m'chipululu, ndipo adamwalira. Mkate wotsika Kumwamba ndi uwu, kuti munthu akadyeko ndi kusamwalira. Mkate wamoyo wotsika Kumwamba Ndine amene. Ngati munthu wina akadyako mkate umene, adzakhala ndi moyo kosatha. Inde, ndipo mkate umene ndidzapatsa Ine, ndiwo thupi langa, ukhale moyo wa dziko lapansi. Pamenepo Ayuda anatetana wina ndi mnzake ndi kunena, Akhoza bwanji ameneyu kutipatsa ife kudya thupi lake? Chifukwa chake Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati simukudya thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa mwazi wake, mulibe moyo mwa inu nokha. Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga ali nao moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza. Pakuti thupi langa ndi chakudya ndithu, ndi mwazi wanga ndi chakumwa ndithu. Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga akhala mwa Ine ndi Ine mwa iye. Monga Atate wamoyo anandituma Ine, ndipo Inenso ndili ndi moyo chifukwa cha Atate; momwemo wondidya Ine, iyeyu adzakhala ndi moyo chifukwa cha Ine. Mkate wotsika Kumwamba ndi umenewu: si monga makolowo, anadya namwalira; iye wakudya mkate umene adzakhala ndi moyo nthawi zonse. Izi ananena m'sunagoge, pakuphunzitsa m'Kapernao. Pamenepo ambiri a ophunzira ake, pakumva izi, anati, Mau awa ndi osautsa; akhoza kumva awa ndani? Koma Yesu podziwa mwa yekha kuti ophunzira ake alikung'ung'udza chifukwa cha ichi, anati kwa iwo, Ichi mukhumudwa nacho? Nanga bwanji ngati mukaona Mwana wa Munthu alikukwera kumene anali kale lomwe? Wopatsa moyo ndi mzimu; thupi silithandiza konse. Mau amene ndalankhula ndi inu ndiwo mzimu, ndi moyo. Koma pali ena mwa inu amene sakhulupirira. Pakuti Yesu anadziwa poyamba amene ali osakhulupirira, ndi amene adzampereka. Ndipo ananena, Chifukwa cha ichi ndinati kwa inu, kuti palibe munthu angathe kudza kwa Ine, koma ngati kupatsidwa kwa iye ndi Atate. Pa ichi ambiri a ophunzira ake anabwerera m'mbuyo, ndipo sanayendeyendenso ndi Iye. Chifukwa chake Yesu anati kwa khumi ndi awiriwo, Nanga inunso mufuna kuchoka? Simoni Petro anamyankha Iye, Ambuye, tidzamuka kwa yani? Inu muli nao mau a moyo wosatha. Ndipo ife tikhulupirira, ndipo tidziwa kuti Inu ndinu Woyera wa Mulungu. Yesu anayankha iwo, Kodi sindinakusankhani khumi ndi awiri, ndipo mwa inu mmodzi ali mdierekezi? Koma adanena za Yudasi, mwana wa Simoni Iskariote, pakuti iye ndiye amene akampereka Iye, ali mmodzi wa khumi ndi awiri. Ndipo zitapita izi Yesu anayendayenda m'Galileya; pakuti sanafune kuyendayenda m'Yudeya, chifukwa Ayuda anafuna kumupha Iye. Koma chikondwerero cha Ayuda cha Misasa, linayandikira. Chifukwa chake abale ake anati kwa Iye, Chokani pano, mumuke ku Yudeya, kuti ophunzira anunso akapenye ntchito zanu zimene muchita. Pakuti palibe munthu achita kanthu mobisika, nafuna yekha kukhala poyera. Ngati muchita izi, dzionetsereni eni nokha kwa dziko lapansi. Pakuti angakhale abale ake sanakhulupirira Iye. Chifukwa chake Yesu ananena nao, Nthawi yanga siinafike; koma nthawi yanu yakonzeka masiku onse. Dziko lapansi silingathe kudana ndi inu; koma Ine lindida popeza Ine ndilichitira umboni, kuti ntchito zake zili zoipa. Kwerani inu kunka kuphwando; sindikwera Ine kuphwando ili tsopano apa; pakuti nthawi yanga siinakwanire. Ndipo m'mene adanena nao zimenezi anakhalabe m'Galileya. Koma pamene abale ake adakwera kunka kuchikondwerero, pomwepo Iyenso anakwera, si poonekera, koma monga mobisalika. Pomwepo Ayuda analikumfuna Iye pachikondwerero, nanena, Ali kuti uja? Ndipo kunali kung'ung'udza kwambiri za Iye m'makamu a anthu; ena ananena, kuti, Ali wabwino; koma ena ananena, Iai, koma asocheretsa khamu la anthuwo. Chinkana anatero panalibe munthu analankhula za Iye poyera, chifukwa cha kuopa Ayuda. Koma pamene padafika pakati pa chikondwerero, Yesu anakwera nalowa m'Kachisi, naphunzitsa. Chifukwa chake Ayuda anazizwa, nanena, Ameneyu adziwa bwanji zolemba, wosaphunzira? Pamenepo Yesu anayankha iwo, nati, Chiphunzitso changa sichili changa, koma cha Iye amene anandituma Ine. Ngati munthu aliyense afuna kuchita chifuniro chake, adzazindikira za chiphunzitsocho, ngati chichokera kwa Mulungu, kapena ndilankhula zochokera kwa Ine ndekha. Iye wolankhula zochokera kwa iye yekha afuna ulemu wa mwini yekha. Iye wakufuna ulemu wa Iye amene anamtuma, yemweyu ali woona, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama. Si Mose kodi anakupatsani inu chilamulo, ndipo kulibe mmodzi mwa inu achita chilamulo? Mufuna kundipha chifukwa ninji? Khamu la anthu linayankha, Muli ndi chiwanda: afuna ndani kukuphani Inu? Yesu anayankha nati kwa iwo, Ndinachita ntchito imodzi, ndipo muzizwa monse. Chifukwa cha ichi Mose anakupatsani inu mdulidwe (si kuti uchokera kwa Mose, koma kwa makolo); ndipo mudula munthu tsiku la Sabata. Ngati munthu alandira mdulidwe tsiku la Sabata, kuti chilamulo cha Mose chingapasulidwe; kodi mundikwiyira Ine, chifukwa ndamchiritsadi munthu tsiku la Sabata? Musaweruze monga maonekedwe, koma weruzani chiweruziro cholungama. Pamenepo ena a iwo a ku Yerusalemu ananena, Kodi suyu amene afuna kumupha? Ndipo taona amalankhula poyera, ndipo sanena kanthu kwa Iye. Kapena kodi akulu adziwa ndithu kuti ndiye Khristu ameneyo? Koma ameneyo tidziwa uko achokera: koma Khristu pamene akadzadza, palibe mmodzi adzadziwa uko achokera. Pamenepo Yesu anafuula m'Kachisi, alikuphunzitsa ndi kunena, Mundidziwa Ine, ndiponso mudziwa uko ndichokera; ndipo sindinadza Ine ndekha, koma Iye wondituma Ine amene inu simumdziwa, ali woona. Ine ndimdziwa Iye; chifukwa ndili wochokera kwa Iye, nandituma Ine Iyeyu. Pamenepo anafuna kumgwira Iye; koma palibe wina anamgwira kumanja, chifukwa nthawi yake siinafike. Koma ambiri a m'khamu la anthu anakhulupirira Iye; ndipo ananena, Pamene Khristu akadza kodi adzachita zizindikiro zambiri zoposa zimene adazichita ameneyo? Afarisi anamva khamu la anthu ling'ung'udza zimenezi za Iye; ndipo ansembe aakulu ndi Afarisi anatuma anyamata kuti akamgwire Iye. Pamenepo Yesu anati, Katsala kanthawi ndili ndi inu, ndipo ndimuka kwa Iye wondituma Ine. Mudzafunafuna Ine, osandipeza; ndipo pomwe ndili Ine, inu simungathe kudzapo. Chifukwa chake Ayuda anati mwa iwo okha, Adzanka kuti uyu kuti ife sitikampeza Iye? Kodi adzamuka kwa Agriki obalalikawo, ndi kuphunzitsa Agriki? Mau awa amene ananena ndi chiyani, Mudzandifunafuna osandipeza Ine: ndipo pomwe ndili Ine, inu simungathe kudzapo? Koma tsiku lomaliza, lalikululo la chikondwerero, Yesu anaimirira nafuula, ndi kunena, Ngati pali munthu akumva ludzu, adze kwa Ine, namwe. Iye wokhulupirira Ine, monga chilembo chinati, Mitsinje ya madzi amoyo idzayenda, kutuluka m'kati mwake. Koma ichi anati za Mzimu, amene iwo akukhulupirira Iye anati adzalandire; pakuti Mzimu panalibe pamenepo, chifukwa Yesu sanalemekezedwe panthawi pomwepo. Pamenepo ena a khamulo pakumva mau awa, ananena, Mneneriyo ndi uyu ndithu. Ena ananena, Uyu ndi Khristu. Koma ena ananena, Kodi Khristu adza kutuluka m'Galileya? Kodi sichinati chilembo kuti Khristu adza kutuluka mwa mbeu ya Davide, ndi kuchokera ku Betelehemu, kumudzi kumene kunali Davide? Kudakhala tsono kusiyana m'khamulo chifukwa cha Iye. Koma ena mwa iwo anafuna kumgwira Iye; koma palibe munthu anamgwira kumanja. Pamenepo anyamatawo anadza kwa ansembe aakulu ndi Afarisi; ndipo iwowa anati kwa iwo, Simunamtenga Iye bwanji? Anyamatawo anayankha, Nthawi yonse palibe munthu analankhula chotero. Pamenepo Afarisi anayankha iwo, Kodi mwasokeretsedwa inunso? Kodi wina wa akulu anakhulupirira Iye, kapena wa Afarisi? Koma khamu ili losadziwa chilamulo, likhala lotembereredwa. Nikodemo ananena kwa iwo, amene uja adadza kwa Iye kale, ali mmodzi wa iwo, Kodi chilamulo chathu chiweruza munthu, osayamba kumva iye, ndi kuzindikira chimene achita? Anayankha nati kwa iye, Kodi iwenso uli wotuluka m'Galileya? Santhula, nuone kuti m'Galileya sanauke mneneri. Ndipo anamuka munthu yense kunyumba yake. Koma Yesu anamuka kuphiri la Azitona. Koma mamawa anadzanso ku Kachisi, ndipo anthu onse anadza kwa Iye; ndipo m'mene anakhala pansi anawaphunzitsa. Koma alembi ndi Afarisi anabwera naye kwa Iye mkazi wogwidwa m'chigololo, ndipo pamene anamuimika iye pakati, ananena kwa Iye, Mphunzitsi, mkazi uyu wagwidwa alimkuchita chigololo. Koma m'chilamulo Mose anatilamula, tiwaponye miyala otere. Chifukwa chake Inu munena chiyani za iye? Koma ichi ananena kuti amuyese Iye, kuti akhale nacho chomneneza Iye. Koma Yesu, m'mene adawerama pansi analemba pansi ndi chala chake. Koma pamene anakhalakhala alikumfunsabe Iye, anaweramuka, nati kwa iwo, Amene mwa inu ali wopanda tchimo, ayambe kumponya mwala. Ndipo m'mene adaweramanso analemba ndi chala chake pansi. Koma iwo, m'mene anatulukamo amodziamodzi, kuyambira akulu, kufikira otsiriza; ndipo Yesu anatsala yekha, ndi mkazi, alikuima pakati. Koma Yesu pamene adaweramuka, anati kwa iye, Mkazi iwe, ali kuti ajawa? Palibe munthu anakutsutsa kodi? Koma iye anati, Palibe, Ambuye. Ndipo Yesu anati, Inenso sindikutsutsa iwe; pita; kuyambira tsopano usachimwenso. Pamenepo Yesu analankhulanso nao, nanena, Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata Ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo. Chifukwa chake Afarisi anati kwa Iye, Muchita umboni wa Inu nokha; umboni wanu suli woona. Anayankha Yesu nati kwa iwo, Ndingakhale ndichita umboni wa Ine ndekha umboni wanga uli woona; chifukwa ndidziwa kumene ndinachokera ndi kumene ndimukako; koma inu simudziwa kumene ndichokera, ndi kumene ndimukako. Inu muweruza monga mwa thupi; Ine sindiweruza munthu. Ndipo ngati ndiweruza Ine, chiweruziro changa chili choona; pakuti sindili pa ndekha, koma Ine ndi Atate amene anandituma Ine. Inde kudalembedwa m'chilamulo chanu kuti umboni wa anthu awiri uli woona. Ine ndine wakuchita umboni wa Ine ndekha, ndipo Atate amene anandituma Ine achita umboni wa Ine. Chifukwa chake ananena ndi Iye, Ali kuti Atate wanu? Yesu anayankha, Simudziwa kapena Ine, kapena Atate wanga; mukadadziwa Ine, mukadadziwanso Atate wanga. Mau awa analankhula m'nyumba yosungiramo chuma cha Mulungu pophunzitsa m'Kachisi; ndipo palibe munthu anamgwira Iye, pakuti nthawi yake siinafike. Pamenepo anatinso kwa iwo; Ndimuka Ine, ndipo mudzandifuna, ndipo m'tchimo lanu mudzafa: kumene ndimukako Ine, simudziwa kudza inu. Chifukwa chake Ayuda anenana, Kodi adzadzipha yekha, pakuti ananena, Kumene ndimukako Ine, simudziwa inu kudza? Ndipo ananena nao, Inu ndinu ochokera pansi; Ine ndine wochokera Kumwamba; inu ndinu a dziko lino lapansi; sindili Ine wa dziko lino lapansi. Chifukwa chake ndinati kwa inu, kuti mudzafa m'machimo kwa inu, kuti mudzafa m'machimo anu, pakuti ngati simukhulupirira kuti Ine ndine, mudzafa m'machimo anu. Pamenepo ananena kwa Iye, Ndinu yani? Yesu anati kwa iwo, Chimene chomwe ndidalankhulanso ndi inu kuyambira pachiyambi. Ndili nazo zambiri zakulankhula ndi zakuweruza za inu; koma wondituma Ine ali woona; ndipo zimene ndazimva kwa Iye, zomwezo ndilankhula kwa dziko lapansi. Sanazindikira iwo kuti analikunena nao za Atate. Chifukwa chake Yesu anati, Pamene mutadzamkweza Mwana wa Munthu, pomwepo mudzazindikira kuti Ine ndine, ndipo sindichita kanthu kwa Ine ndekha, koma monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi. Ndipo wondituma Ine ali ndi Ine; sanandisiye Iye pa ndekha; chifukwa ndichita Ine zimene zimkondweretsa Iye nthawi zonse. Pakulankhula Iye zimenezi ambiri anakhulupirira Iye. Chifukwa chake Yesu ananena kwa Ayuda aja adakhulupirira Iye, Ngati mukhala inu m'mau anga, muli ophunzira anga ndithu; ndipo mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani. Anamyankha iye, Tili mbeu ya Abrahamu, ndipo sitinakhala akapolo a munthu nthawi iliyonse; munena bwanji, Mudzayesedwa afulu? Yesu anayankha iwo, nati, Indetu, indetu, ndinena kwa inu kuti yense wakuchita tchimo ali kapolo wa chimolo. Koma kapolo sakhala m'nyumba nthawi yonse; mwana ndiye akhala nthawi yonse. Chifukwa chake ngati Mwana adzakuyesani inu aufulu, mudzakhala mfulu ndithu. Ndidziwa kuti muli mbeu ya Abrahamu; koma mufuna kundipha Ine, chifukwa mau anga alibe malo mwa inu. Zimene ndinaona Ine kwa Atate, ndilankhula; ndipo inunso muchita chimene mudamva kwa atate wanu. Anayankha nati kwa iye, Atate wathu ndiye Abrahamu. Yesu ananena nao, Ngati muli ana a Abrahamu, mukadachita ntchito za Abrahamu. Koma tsopano mufuna kundipha Ine, ndine munthu amene ndinalankhula ndi inu choonadi, chimene ndinamva kwa Mulungu; ichi Abrahamu sanachite. Inu muchita ntchito za atate wanu. Anati kwa Iye, Sitinabadwa ife m'chigololo; tili naye Atate mmodzi ndiye Mulungu. Yesu anati kwa iwo, Mulungu akadakhala Atate wanu, mukadakonda Ine; pakuti Ine ndinatuluka, ndi kuchokera kwa Mulungu; pakuti sindinadza kwa Ine ndekha, koma Iyeyu anandituma Ine. Simuzindikira malankhulidwe anga chifukwa ninji? Chifukwa simungathe kumva mau anga. Inu muli ochokera mwa atate wanu mdierekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaime m'choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza. Koma Ine, chifukwa ndinena choonadi, simukhulupirira Ine. Ndani mwa inu anditsutsa Ine za tchimo? Ngati ndinena choonadi, simundikhulupirira Ine chifukwa ninji? Iye wochokera kwa Mulungu amva zonena za Mulungu; inu simumva chifukwa chakuti simuli a kwa Mulungu. Ayuda anayankha nati kwa Iye, Kodi sitinenetsa kuti Inu ndinu Msamariya, ndipo muli ndi chiwanda? Yesu anayankha, Ndilibe chiwanda Ine; koma ndilemekeza Atate wanga, ndipo inu mundipeputsa. Koma Ine sinditsata ulemerero wanga; alipo woutsata ndi wakuweruza. Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Munthu akasunga mau anga, sadzaona imfa nthawi yonse. Ayuda anati kwa Iye, Tsopano tazindikira kuti muli ndi chiwanda. Abrahamu anamwalira, ndi aneneri; ndipo Inu munena, Munthu akasunga mau anga, sadzalawa imfa kunthawi yonse. Kodi Inu ndinu wamkulu ndi atate wathu Abrahamu, amene anamwalira? Ndipo aneneri anamwalira: mudziyesera nokha muli yani? Yesu anayankha, Ngati Ine ndidzilemekeza ndekha, ulemerero wanga uli chabe; Atate wanga ndiye wondilemekeza Ine; amene munena za Iye, kuti ndiye Mulungu wanu; ndipo inu simunamdziwa Iye; koma Ine ndimdziwa Iye; ndipo ngati ndinena kuti sindimdziwa Iye, ndidzakhala wonama chimodzimodzi inu; koma ndimdziwa Iye, ndipo ndisunga mau ake. Atate wanu Abrahamu anakondwera kuona tsiku langa; ndipo anaona nasangalala. Ayuda pamenepo anati kwa Iye, Simunafikire zaka makumi asanu, ndipo munaona Abrahamu kodi? Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, asanayambe kukhala Abrahamu ndipo Ine ndilipo. Pamenepo anatola miyala kuti amponye Iye; koma Yesu anabisala, natuluka m'Kachisi. Ndipo popita, anaona munthu ali wosaona chibadwire. Ndipo ophunzira ake anamfunsa Iye, nanena, Rabi, anachimwa ndani, ameneyo, kapena atate wake ndi amake, kuti anabadwa wosaona? Yesu anayankha, Sanachimwe ameneyo, kapena atate wake ndi amake; koma kuti ntchito za Mulungu zikaonetsedwe mwa iye. Tiyenera kugwira ntchito za Iye wondituma Ine, pokhala pali msana; ukudza usiku pamene palibe munthu angakhoze kugwira ntchito. Pakukhala Ine m'dziko lapansi, ndili kuunika kwa dziko lapansi. Pamene ananena izi, analavula pansi, nakanda thope ndi malovuwo, napaka thopelo m'maso, nati kwa iye, Muka, kasambe m'thamanda la Siloamu (ndilo losandulika, Wotumidwa). Pamenepo anachoka, nasamba, nabwera alikuona. Chifukwa chake anzake ndi iwo adamuona kale, kuti anali wopemphapempha, ananena, Kodi si uyu uja wokhala ndi kupemphapempha? Ena ananena, kuti, Ndiyeyu; ena ananena, Iai, koma afanana naye. Iyeyu anati, Ndine amene. Pamenepo anenana ndi iye, Nanga maso ako anatseguka bwanji? Iyeyu anayankha, Munthuyo wotchedwa Yesu anakanda thope, napaka m'maso mwanga, nati, kwa ine, Muka ku Siloamu kasambe; chifukwa chake ndinachoka, ndipo m'mene ndinasamba ndinapenya. Ndipo anati kwa iye, Ali kuti Iyeyo? Anena, Sindidziwa ine. Anapita naye amene anali wosaona kale kwa Afarisi. Koma tsikulo ndi la Sabata limene Yesu anakanda thope, namtsegulira iye maso ake. Pamenepo ndipo Afarisi anamfunsanso, umo anapenyera. Ndipo anati kwa iwo, Anapaka thope m'maso mwanga, ndinasamba, ndipo ndipenya. Ena pamenepo mwa Afarisi ananena, Munthu uyu sachokera kwa Mulungu, chifukwa sasunga Sabata. Koma ena ananena, Munthu ali wochimwa akhoza bwanji kuchita zizindikiro zotere? Ndipo panali kutsutsana mwa iwo. Pamenepo ananenanso kwa wosaonayo, Iwe unenanji za Iye, popeza anakutsegulira maso ako? Koma iye anati, Ali Mneneri. Chifukwa chake Ayuda sanakhulupirire za iye, kuti anali wosaona, napenya, kufikira kumene adaitana atate wake ndi amake a iye wopenya; nawafunsa iwo, nanena, Kodi uyu ndi mwana wanu, amene inu munena kuti anabadwa wosaona? Ndipo apenya bwanji tsopano? Atate wake ndi amake anayankha nati, Tidziwa kuti uyu ndi mwana wathu, ndi kuti anabadwa wosaona; koma sitidziwa uno apenyera tsopano; kapena sitimdziwa mene anamtsegulira pamaso pake; mumfunse iye; ali wamsinkhu; adzalankhula mwini za iye yekha. Izi ananena atate wake ndi amake, chifukwa anaopa Ayuda; pakuti Ayuda adapangana kale, kuti ngati munthu aliyense adzamvomereza Iye kuti ndiye Khristu, akhale woletsedwa m'sunagoge. Chifukwa cha ichi atate wake ndi amake anati, Ali wamsinkhu; mumfunse iye. Pamenepo anamuitana kachiwiri munthuyo amene anali wosaona, nati kwa iye, Lemekeza Mulungu; tidziwa kuti munthuyo ali wochimwa. Pamenepo iyeyu anayankha, Ngati ali wochimwa, sindidziwa; chinthu chimodzi ndichidziwa, pokhala ndinali wosaona, tsopano ndipenya. Chifukwa chake anati kwa iye, Anakuchitira iwe chiyani? Anakutsegulira iwe maso bwanji? Iye anayankha iwo, Ndinakuuzani kale, ndipo simunamva; mufuna kumvanso bwanji? Kodi inunso mufuna kukhala ophunzira ake? Ndipo anamlalatira iye, nati, Ndiwe wophunzira wa Iyeyu, ife ndife ophunzira a Iyeyu, ife ndife ophunzira a Mose. Tidziwa ife kuti Mulungu analankhula ndi Mose; koma sitidziwa kumene achokera ameneyo. Munthuyu anayankha nati kwa iwo, Pakuti chozizwa chili m'menemo, kuti inu simudziwa kumene achokera, ndipo ananditsegulira maso anga. Tidziwa kuti Mulungu samvera ochimwa. Koma ngati munthu aliyense akhala wopembedza Mulungu nachita chifuniro chake, amvera ameneyo. Kuyambira pachiyambi sikunamveka kuti wina anatsegulira maso munthu wosaona chibadwire. Ngati uyu sanachokera kwa Mulungu, sakadakhoza kuchita kanthu. Anayankha nati kwa iye, Wabadwa iwe konse m'zoipa, ndipo iwe utiphunzitse ife kodi? Ndipo anamtaya kunja. Yesu anamva kuti adamtaya kunja; ndipo pakumpeza iye, anati, Kodi ukhulupirira Mwana wa Munthu? Iyeyu anayankha nati, Ndipo ndani Iye, Ambuye, kuti ndimkhulupirire Iye? Yesu anati kwa iye, Wamuona Iye, ndiponso wakulankhula ndi iwe ndi Iyeyo. Koma iye anati, Ndikhulupirira, Ambuye; ndipo anamgwadira Iye. Ndipo Yesu anati, Kudzaweruza ndadza Ine kudziko lino lapansi, kuti iwo osapenya apenye; ndi kuti iwo akupenya akhale osaona. Ndipo Afarisi ena akukhala ndi Iye anamva izi, nati kwa Iye, Kodi ifenso ndife osaona? Yesu anati kwa iwo, Mukadakhala osaona simukadakhala nalo tchimo; koma tsopano munena, kuti, Tipenya: tchimo lanu likhala. Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wosalowa m'khola la nkhosa pakhomo, koma akwerera kwina, iyeyu ndiye wakuba ndi wolanda. Koma iye wakulowera pakhomo, ndiye mbusa wa nkhosa. Iyeyu, wapakhomo amtsegulira ndi nkhosa zimva mau ake; ndipo aitana nkhosa za iye yekha maina ao, nazitsogolera kunja. Pamene adatulutsa zonse nkhosa zimtsata iye; chifukwa zidziwa mau ake. Koma mlendo sizidzamtsata, koma zidzamthawa; chifukwa sizidziwa mau a alendo. Fanizo ili Yesu ananena kwa iwo; koma sanazindikira zimene Yesu analikulankhula nao. Chifukwa chake Yesu ananenanso nao, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ine ndine khomo la nkhosa. Onse amene anadza m'tsogolo mwa Ine ali akuba, ndi olanda: koma nkhosa sizinamva iwo. Ine ndine khomo; ngati wina alowa ndi Ine, adzapulumutsidwa, nadzalowa, nadzatuluka, nadzapeza busa. Siikudza mbala, koma kuti ikabe, ndi kupha, ndi kuononga. Ndadza Ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nao wochuluka. Ine ndine Mbusa Wabwino; mbusa wabwino ataya moyo wake chifukwa cha nkhosa. Wolipidwa amene sakhala mbusa, amene nkhosa sizili zake za yekha, aona mmbulu ulinkudza, nasiya nkhosazo, nathawa; ndipo mmbulu uzikwatula, nuzibalalitsa; chifukwa ali wolipidwa, ndipo sasamala nkhosa. Ine ndiye Mbusa Wabwino; ndipo ndizindikira zanga, ndi zanga zindizindikira Ine, monga Atate andidziwa Ine, ndi Ine ndimdziwa Atate; ndipo nditaya moyo wanga chifukwa cha nkhosa. Ndipo nkhosa zina ndili nazo, zimene sizili za khola ili; izinso ndiyenera kuzitenga, ndipo zidzamva mau anga; ndipo zidzakhala gulu limodzi, mbusa mmodzi. Chifukwa cha ichi Atate andikonda Ine, chifukwa nditaya Ine moyo wanga, kuti ndikautengenso. Palibe wina andichotsera uwu, koma ndiutaya Ine ndekha. Ndili nayo mphamvu yakuutaya, ndi mphamvu ndili nayo yakuutenganso; lamulo ili ndinalandira kwa Atate wanga. Panakhalanso kutsutsana pakati pa Ayuda chifukwa cha mau awa. Koma ambiri mwa iwo ananena, Ali ndi chiwanda, nachita misala; mukumva Iye bwanji? Ena ananena, Mau awa sali a munthu wogwidwa chiwanda. Kodi chiwanda chikhoza kumtsegulira maso wosaona? Koma kunali phwando la kukonzetsanso m'Yerusalemu; nyengoyo ndi yachisanu. Ndipo Yesu analikuyendayenda m'Kachisi m'khonde la Solomoni. Pamenepo Ayuda anamzungulira Iye, nanena ndi Iye, Kufikira liti musinkhitsasinkhitsa moyo wathu? Ngati Inu ndinu Khristu, tiuzeni momveka. Yesu anayankha iwo, Ndakuuzani, ndipo simukhulupirira. Ntchitozi ndidzichita Ine m'dzina la Atate wanga, zimenezi zindichitira umboni. Koma inu simukhulupirira, chifukwa simuli a mwa nkhosa zanga. Nkhosa zanga zimva mau anga, ndipo Ine ndizizindikira, ndipo zinditsata Ine. Ndipo Ine ndizipatsa moyo wosatha; ndipo sizidzaonongeka kunthawi yonse, ndipo palibe munthu adzazikwatula m'dzanja langa. Atate wanga, amene anandipatsa izo, ali wamkulu ndi onse; ndipo palibe wina ngathe kuzikwatula m'dzanja la Atate. Ine ndi Atate ndife amodzi. Ayuda anatolanso miyala kuti amponye Iye. Yesu anayankha iwo, Ndakuonetsani inu ntchito zabwino zambiri za kwa Atate; chifukwa cha ntchito yiti ya izo mundiponya miyala? Ayuda anamyankha Iye, Chifukwa cha ntchito yabwino sitikuponyani miyala, koma chifukwa cha mwano; ndi kuti Inu, muli munthu, mudziyesera nokha Mulungu. Yesu anayankha iwo, Kodi sikulembedwa m'chilamulo chanu, Ndinati Ine, Muli milungu? Ngati anawatcha milungu iwo amene mau a Mulungu anawadzera (ndipo cholemba sichingathe kuthyoka), kodi inu munena za Iye, amene Atate anampatula namtuma kudziko lapansi, Uchita mwano; chifukwa ndinati, Ndili Mwana wa Mulungu? Ngati sindichita ntchito za Atate wanga, musakhulupirira Ine. Koma ngati ndichita, mungakhale simukhulupirira Ine, khulupirirani ntchitozo; kuti mukadziwe ndi kuzindikira kuti Atate ali mwa Ine, ndi Ine mwa Atate. Anafunanso kumgwira Iye; ndipo anapulumuka m'dzanja lao. Ndipo anachoka kunkanso tsidya lija la Yordani, kumalo kumene kunali Yohane analikubatiza poyamba paja; ndipo anakhala komweko. Ndipo ambiri anadza kwa Iye; nanena kuti, Sanachita chizindikiro Yohane; koma zinthu zilizonse Yohane ananena za Iye zinali zoona. Ndipo ambiri anakhulupirira Iye komweko. Koma panali munthu wodwala, Lazaro wa ku Betaniya, wa m'mudzi wa Maria ndi mbale wake Marita. Koma ndiye Maria uja anadzoza Ambuye ndi mafuta onunkhira bwino, napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake, amene mlongo wake Lazaro anadwala. Pamenepo alongo ake anatumiza kwa Iye, nanena, Ambuye, onani, amene mumkonda adwala. Koma Yesu pamene anamva, anati, Kudwala kumene sikuli kwa imfa, koma chifukwa cha ulemerero wa Mulungu, kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe nako. Koma Yesu anakonda Marita, ndi mbale wake, ndi Lazaro. Chifukwa chake pamene anamva kuti anadwala, anakhala pamenepo pa malo pomwepo masiku awiri. Ndipo pambuyo pake ananena kwa ophunzira ake, Tiyeni tipitenso ku Yudeya. Ophunzira ananena ndi Iye, Rabi, Ayuda analikufuna kukuponyani miyala tsopano apa; ndipo munkanso komweko kodi? Yesu anayankha, Kodi sikuli maora khumi ndi awiri usana? Ngati munthu ayenda usana sakhumudwa, chifukwa apenya kuunika kwa dziko lino lapansi. Koma ngati munthu ayenda usiku, akhumudwa, chifukwa mulibe kuunika mwa iye. Izi anati, ndipo zitatha izi ananena nao, Lazaro bwenzi lathu ali m'tulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo take. Chifukwa chake ophunzira ake anati kwa Iye, Ambuye, ngati ali m'tulo adzachira. Koma Yesu adanena za imfa yake; koma iwowa anayesa kuti ananena za mpumulo wa tulo. Pamenepo Yesu anati kwa iwo momveka, Lazaro wamwalira. Ndipo ndikondwera chifukwa cha inu kuti kunalibe Ine komweko, chakuti mukakhulupirire; koma tiyeni, tipite kwa iye. Pamenepo Tomasi, wotchedwa Didimo, anati kwa ophunzira anzake, Tipite ifenso kuti tikafere naye pamodzi. Ndipo pamene Yesu anadza, anapeza kuti pamenepo atakhala m'manda masiku anai. Koma Betaniya anali pafupi pa Yerusalemu, nthawi yake yonga ya mastadiya khumi ndi asanu; koma ambiri a mwa Ayuda adadza kwa Marita ndi Maria, kudzawatonthoza mtima pa mlongo wao. Pamenepo Marita, pakumva kuti Yesu alinkudza, anamuka kukakomana ndi Iye; koma Maria anakhalabe m'nyumba. Ndipo Marita anati kwa Yesu, Ambuye, mukadakhala kuno mlongo wanga sakadafa. Koma ngakhale tsopano ndidziwa kuti zinthu zilizonse mukapempha Mulungu, adzakupatsani Mulungu. Yesu ananena naye, Mlongo wako adzauka. Marita ananena ndi Iye, Ndidziwa kuti adzauka m'kuuka tsiku lomaliza. Yesu anati kwa iye, Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo; ndipo yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthawi yonse. Kodi ukhulupirira ichi? Ananena ndi Iye, Inde Ambuye; ndakhulupirira ine kuti Inu ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu, wakudza m'dziko lapansi. Ndipo m'mene anati ichi anachoka naitana Maria mbale wake m'tseri, ndi kuti, Wafika Mphunzitsi, akuitana iwe. Koma iyeyo, pakumva, ananyamuka msanga, nadza kwa Iye. (Koma Yesu sanafike kumudzi, koma anali pamalo pomwe Marita adakomana ndi Iye.) Pamenepo Ayuda okhala naye m'nyumba, ndi kumtonthoza iye, pakuona Maria ananyamuka msanga, natuluka, namtsata iye, ndi kuyesa kuti amuka kumanda kukalira komweko. Pomwepo Maria, pofika pamene panali Yesu, m'mene anamuona Iye, anagwa pa mapazi ake, nanena ndi Iye, Ambuye, mukadakhala kuno Inu, mlongo wanga sakadamwalira. Pamenepo Yesu, pakumuona iye alikulira, ndi Ayuda akumperekeza iye alikulira, anadzuma mumzimu, navutika mwini, nati, Mwamuika iye kuti? Ananena ndi Iye, Ambuye, tiyeni mukaone. Yesu analira. Chifukwa chake Ayuda ananena, Taonani, anamkondadi! Koma ena mwa iwo anati, Kodi uyu wotsegulira maso wosaona uja, sanakhoza kodi kuchita kuti sakadafa ameneyunso? Pamenepo Yesu, ndi kudzumanso mwa Iye yekha anadza kumanda. Koma panali phanga, ndipo mwala unaikidwa pamenepo. Yesu ananena, Chotsani mwala. Marita, mlongo wake wa womwalirayo, ananena ndi Iye, Ambuye, adayamba kununkha: pakuti wagona masiku anai. Yesu ananena naye, Kodi sindinati kwa iwe, kuti, ngati ukhulupirira, udzaona ulemerero wa Mulungu? Pomwepo anachotsa mwala. Koma Yesu anakweza maso ake kupenya kumwamba nati, Atate, ndiyamika Inu kuti munamva Ine. Koma ndadziwa Ine kuti mumandimva Ine nthawi zonse; koma chifukwa cha khamu la anthu alikuimirira pozungulira ndinanena ichi, kuti akhulupirire kuti Inu munandituma Ine. Ndipo m'mene adanena izi, anafuula ndi mau akulu, Lazaro, tuluka. Ndipo womwalirayo anatuluka womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za kumanda; ndi nkhope yake inazingidwa ndi mlezo. Yesu ananena nao, Mmasuleni iye, ndipo mlekeni amuke. Chifukwa chake ambiri a mwa Ayuda amene anadza kwa Maria, m'mene anaona chimene anachita, anakhulupirira Iye. Koma ena a mwa iwo anamuka kwa Afarisi, nawauza zimene Yesu adazichita. Pamenepo ansembe aakulu ndi Afarisi anasonkhanitsa akulu, nanena, Titani ife? Chifukwa munthu uyu achita zizindikiro zambiri. Ngati timleka Iye kotero, onse adzakhulupirira Iye; ndipo adzadza Aroma nadzachotsa malo athu ndi mtundu wathu. Koma wina mmodzi wa mwa iwo, Kayafa, wokhala mkulu wa ansembe chaka chomwecho anati kwa iwo, Simudziwa kanthu konse inu, kapena simuganiza kuti nkokoma kwa inu kuti munthu mmodzi afere anthu, ndi kuti mtundu wonse usaonongeke. Koma ichi sananena kwa iye yekha; koma pokhala mkulu wa ansembe chaka chomwecho ananenera kuti Yesu akadzafera mtunduwo; ndipo si chifukwa cha mtunduwo wokha ai, koma kuti akasonkhanitse pamodzi ana a Mulungu akubalalikawo. Chifukwa chake, kuyambira tsiku lomwelo anapangana kuti amuphe Iye. Chifukwa chake Yesu sanayandeyendanso poonekera mwa Ayuda, koma anachokapo kunka kudziko loyandikira chipululu, kumudzi dzina lake Efuremu; nakhala komweko pamodzi ndi ophunzira ake. Koma Paska wa Ayuda anali pafupi; ndipo ambiri anakwera kunka ku Yerusalemu kuchoka ku milaga, usanafike Paska, kukadziyeretsa iwo okha. Pamenepo analikumfuna Yesu, nanena wina ndi mnzake poimirira iwo m'Kachisi, Muyesa bwanji inu, sadzadza kuchikondwerero kodi? Koma ansembe aakulu ndi Afarisi adalamula kuti, munthu wina akadziwa pokhala Iye, aulule, kuti akamgwire Iye. Pomwepo anatsala masiku asanu ndi limodzi asanafike Paska, Yesu anadza ku Betaniya kumene kunali Lazaro, amene Yesu adamuukitsa kwa akufa. Ndipo anamkonzera Iye chakudya komweko; ndipo Marita anatumikira; koma Lazaro anali mmodzi wa iwo akuseama pachakudya pamodzi ndi Iye. Pamenepo Maria m'mene adatenga muyeso umodzi wa mafuta onunkhira bwino a narido weniweni a mtengo wake wapatali, anadzoza mapazi a Yesu, napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake; ndipo nyumba inadzazidwa ndi mnunkho wake wa mafutawo. Koma Yudasi Iskariote, mmodzi wa ophunzira ake, amene adzampereka Iye, ananena, Nanga mafuta onunkhira awa sanagulitsidwa chifukwa ninji ndi marupiya atheka mazana atatu, ndi kupatsidwa kwa osauka? Koma ananena ichi si chifukwa analikusamalira osauka, koma chifukwa anali mbala, ndipo pokhala nalo thumba, amaba zoikidwamo. Pamenepo Yesu anati, Mleke iye, pakuti anachisungira ichi tsiku la kuikidwa kwanga. Pakuti osauka muli nao pamodzi ndi Ine nthawi zonse; koma simuli ndi Inu nthawi zonse. Pamenepo khamu lalikulu la Ayuda linadziwa kuti ali pomwepo; ndipo anadza, si chifukwa cha Yesu yekha, koma kuti adzaone Lazaro, amene adamuukitsa kwa akufa. Koma ansembe aakulu anapangana kuti akaphe Lazaronso; pakuti ambiri a Ayuda anachoka chifukwa cha iye, nakhulupirira Yesu. M'mawa mwake khamu lalikulu la anthu amene adadza kuchikondwerero, pakumva kuti Yesu alinkudza ku Yerusalemu, anatenga makwata a kanjedza, natuluka kukakomana ndi Iye, nafuula, Hosana; wolemekezeka Iye wakudza m'dzina la Ambuye, ndiye mfumu ya Israele. Koma Yesu, m'mene adapeza kabulu anakhala pamenepo; monga mulembedwa: Usaope, mwana wamkazi wa Ziyoni; taona mfumu yako idza wokhala pa mwana wa bulu. Izi sanazidziwa ophunzira ake poyamba; koma pamene Yesu analemekezedwa, pamenepo anakumbukira kuti izi zinalembedwa za Iye, ndi kuti adamchitira Iye izi. Pamenepo khamulo limene linali pamodzi ndi Iye, m'mene anaitana Lazaro kutuluka kumanda, namuukitsa kwa akufa, anachita umboni. Chifukwa cha ichinso khamulo linadza kudzakomana ndi Iye, chifukwa anamva kuti Iye adachita chizindikiro ichi. Chifukwa chake Afarisi ananena wina ndi mnzake, Muona kuti simupindula kanthu konse; onani dziko litsata pambuyo pake pa Iye. Koma panali Agriki ena mwa iwo akukwera kunka kukalambira pachikondwerero. Ndipo iwo anadza kwa Filipo wa ku Betsaida wa m'Galileya, namfunsa iye, ndi kuti, Mbuye, tifuna kuona Yesu. Filipo anadza nanena kwa Andrea; nadza Andrea ndi Filipo, nanena ndi Yesu. Koma Yesu anayankha iwo, nati, Yafika nthawi, kuti Mwana wa Munthu alemekezedwe. Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati mbeu ya tirigu siigwa m'nthaka, nifa, ikhala pa yokha iyo; koma ngati ifa, ibala chipatso chambiri. Iye wokonda moyo wake adzautaya; ndipo wodana ndi moyo wake m'dziko lino lapansi adzausungira kumoyo wosatha. Ngati wina anditumikira Ine, anditsate; ndipo kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga. Ngati wina anditumikira Ine, Atate adzamchitira ulemu iyeyu. Moyo wanga wavutika tsopano; ndipo ndidzanena chiyani? Atate, ndipulumutseni Ine kunthawi iyi. Koma chifukwa cha ichi ndinadzera nthawi iyi. Atate, lemekezani dzina lanu. Pomwepo adadza mau ochokera Kumwamba, Ndalilemekeza, ndipo ndidzalilemekezanso. Chifukwa chake khamu la anthu akuimirirako, ndi kuwamva ananena kuti kwagunda. Ena ananena, Mngelo walankhula ndi Iye. Yesu anayankha nati, Mau awa sanafika chifukwa cha Ine, koma cha inu. Tsopano pali kuweruza kwa dziko ili lapansi; mkulu wa dziko ili lapansi adzatayidwa kunja tsopano. Ndipo Ine, m'mene ndikakwezedwa kudziko, ndidzakoka anthu onse kwa Ine ndekha. Koma ananena ichi ndi kuzindikiritsa imfa yanji akuti adzafa nayo. Pamenepo khamulo linayankha Iye, Tidamva ife m'chilamulo kuti Khristu akhala kunthawi yonse; ndipo Inu munena bwanji, kuti Mwana wa Munthu ayenera kukwezedwa? Mwana wa Munthu amene ndani? Pamenepo Yesu anati kwa iwo, Katsala kanthawi kakang'ono ndipo kuunika kuli mwa inu. Yendani pokhala muli nako kuunika, kuti mdima sungakupezeni; ndipo woyenda mumdima sadziwa kumene amukako. Pokhala muli nako kuunika, khulupirirani kuunikako, kuti mukakhale ana a kuunikako. Izi Yesu analankhula, nachoka nawabisalira. Koma angakhale adachita zizindikiro zambiri zotere pamaso pao iwo sanakhulupirira Iye; kuti mau a Yesaya mneneri akakwaniridwe, amene anati, Ambuye, wakhulupirira ndani kulalikira kwathu? Ndipo mkono wa Ambuye wavumbulutsidwa kwa yani? Chifukwa cha ichi sanathe kukhulupirira, pakuti Yesaya anatinso, Wadetsa maso ao, naumitsa mtima wao; kuti angaone ndi maso, angazindikire ndi mtima, nangatembenuke, ndipo ndingawachiritse. Izi anati Yesaya, chifukwa anaona ulemerero wake; nalankhula za Iye. Kungakhale kotero, ambiri a mwa akulu anakhulupirira Iye; koma chifukwa cha Afarisi sanavomereza, kuti angaletsedwe m'sunagoge, pakuti anakonda ulemerero wa anthu koposa ulemerero wa Mulungu. Koma Yesu anafuula nati, Iye wokhulupirira Ine, sakhulupirira Ine, koma Iye wondituma Ine. Ndipo wondiona Ine aona amene anandituma Ine. Ndadza Ine kuunika kudziko lapansi, kuti yense wokhulupirira Ine asakhale mumdima. Ndipo ngati wina akumva mau anga, ndi kusawasunga, Ine sindimweruza; pakuti sindinadza kudzaweruza dziko lapansi, koma kuti ndipulumutse dziko lapansi. Iye amene akaniza Ine, ndi kusalandira mau anga, ali naye womweruza iye, mau amene ndalankhula, iwowa adzamweruza tsiku lomaliza. Pakuti sindinalankhula mwa Ine ndekha; koma Atate wondituma Ine, yemweyu anandipatsa Ine lamulo, limene ndikanene, ndi limene ndikalankhule. Ndipo ndidziwa kuti lamulo lake lili moyo wosatha; chifukwa chake zimene ndilankhula, monga momwe Atate wanena ndi Ine, momwemo ndilankhula. Koma pasanafike chikondwerero la Paska, Yesu, podziwa kuti nthawi yake idadza yakuchoka kutuluka m'dziko lino lapansi, kunka kwa Atate, m'mene anakonda ake a Iye yekha a m'dziko lapansi, anawakonda kufikira chimaliziro. Ndipo pokhala pamgonero, mdierekezi adatha kuika mu mtima wake wa Yudasi mwana wa Simoni Iskariote, kuti akampereke Iye, Yesu, podziwa kuti Atate adampatsa Iye zonse m'manja mwake, ndi kuti anachokera kwa Mulungu, namuka kwa Mulungu, ananyamuka pamgonero, navula malaya ake; ndipo m'mene adatenga chopukutira, anadzimanga m'chuuno. Pomwepo anathira madzi m'nsambidwe, nayamba kusambitsa mapazi a ophunzira ake, ndi kuwapukuta ndi chopukutira, chimene anadzimanga nacho. Anadza pomwepo kwa Simoni Petro. Iyeyu ananena ndi Iye, Ambuye, kodi Inu mundisambitsa ine mapazi? Yesu anayankha nati kwa iye, Chimene ndichita Ine suchidziwa tsopano; koma udzadziwa m'tsogolo mwake. Petro ananena ndi Iye, Simudzasambitsa mapazi anga kunthawi yonse. Yesu anamyankha iye, Ngati sindikusambitsa iwe ulibe cholandira pamodzi ndi Ine. Simoni Petro ananena ndi Iye, Ambuye, si mapazi anga okha, komanso manja ndi mutu. Yesu ananena naye, Amene anatha kusamba alibe kusowa koma kusamba mapazi, koma ayera monse: ndipo inu ndinu oyera, koma si nonse ai. Pakuti anadziwa amene adzampereka Iye; chifukwa cha ichi anati, Simuli oyera nonse. Pamenepo, atatha Iye kusambitsa mapazi ao, ndi kutenga malaya ake, anaseamanso, nati kwa iwo, Nanga chimene ndakuchitirani inu, muchizindikira kodi? Inu munditcha Ine Mphunzitsi, ndi Ambuye: ndipo munena bwino; pakuti ndine amene. Chifukwa chake, ngati Ine Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi wina ndi mnzake. Pakuti ndakupatsani inu chitsanzo, kuti, monga Ine ndakuchitirani inu, inunso muchite. Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wake; kapena mtumwi sali wamkulu ndi womtuma iye. Ngati mudziwa izi, odala inu ngati muzichita. Sindinena za inu nonse; ndidziwa amene ndawasankha: koma kuti cholemba chikwaniridwe, Iye wakudya mkate wanga anatsalimira pa Ine chidendene chake. Kuyambira tsopano ndinena kwa inu, chisadachitike, kuti pamene chitachitika, mukakhulupirire kuti ndine amene. Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wolandira amene aliyense ndimtuma, andilandira Ine; koma wolandira Ine alandira wondituma Ine. Yesu m'mene adanena izi, anavutika mumzimu, nachita umboni, nati, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, kuti mmodzi wa inu adzandipereka Ine. Ophunzira analikupenyana wina kwa mnzake, ndi kusinkhasinkha kuti ananena za yani. Koma mmodzi wa ophunzira ake, amene Yesu anamkonda, analikutsamira pa chifuwa cha Yesu. Pamenepo Simoni Petro anamkodola nanena naye, Utiuze ndiye yani amene anena za iye. Iyeyu potsamira pomwepo, pa chifukwa cha Yesu, anena ndi Iye, Ambuye, ndiye yani? Ndipo Yesu anayankha, Ndi iyeyu, amene Ine ndidzamsunsira nthongo ndi kumpatsa. Pamenepo, m'mene anasunsa nthongo anaitenga naipatsa Yudasi mwana wa Simoni Iskariote. Ndipo pambuyo pake pa nthongoyo, Satana analowa mwa iyeyu. Pamenepo Yesu ananena naye, Chimene uchita, chita msanga. Koma palibe mmodzi wa iwo akuseamako anadziwa chimene anafuna, poti atere naye. Pakuti popeza Yudasi anali nalo thumba, ena analikuyesa kuti Yesu ananena kwa iye, Gula zimene zitisowa pachikondwerero; kapena, kuti apatse kanthu kwa aumphawi. Pamenepo iyeyo m'mene adalandira nthongo, anatuluka pomwepo. Koma kunali usiku. Tsono m'mene adatuluka, Yesu ananena, Tsopano walemekezeka Mwana wa Munthu, ndipo Mulungu walemekezedwa mwa Iye; ndipo Mulungu adzamlemekeza Iye mwa Iye yekha, adzamlemekeza Iye tsopano apa. Tiana, katsala kanthawi ndikhala ndi inu. Mudzandifunafuna Ine; ndipo monga ndinanena kwa Ayuda, kuti kumene ndinkako Ine, inu simungathe kudza, momwemo ndinena kwa inu tsopano. Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake. Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli ophunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake. Simoni Petro anena ndi Iye, Ambuye, mumuka kuti? Yesu anayankha, Kumene ndimukako sungathe kunditsata Ine tsopano; koma, udzanditsata bwino lomwe. Petro ananena ndi Iye, Ambuye, sindingathe kukutsatani Inu tsopano chifukwa ninji? Ndidzataya moyo wanga chifukwa cha Inu. Yesu anayankha, Moyo wako kodi udzautaya chifukwa cha Ine? Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, Asanalire tambala udzandikana Ine katatu. Mtima wanu usavutike; mukhulupirira Mulungu, khulupirirani Inenso. M'nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. Ngati sikudali kutero, ndikadakuuzani inu; pakuti ndipita kukukonzerani inu malo. Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso. Ndipo kumene ndinkako Ine, mudziwa njira yake. Tomasi ananena ndi Iye, Ambuye, sitidziwa kumene munkako; tidziwa njira bwanji? Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine. Mukadazindikira Ine mukadadziwa Atate wanganso; kuyambira tsopano mumzindikira Iye, ndipo mwamuona Iye. Filipo ananena ndi Iye, Ambuye, tionetsereni ife Atate, ndipo chitikwanira. Yesu ananena naye, Kodi ndili ndi inu nthawi yaikulu yotere, ndipo sunandizindikira, Filipo? Iye amene wandiona Ine waona Atate; unena iwe bwanji, Mutionetsere Atate? Sukhulupirira kodi kuti ndili Ine mwa Atate, ndi Atate ali mwa Ine? Mau amene ndinena Ine kwa inu sindilankhula kwa Ine ndekha; koma Atate wokhala mwa Ine achita ntchito zake. Khulupirirani Ine, kuti Ine ndili mwa Atate ndi Atate ali mwa Ine; koma ngati si chomwecho, khulupirirani Ine chifukwa cha ntchito zomwe. Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Wokhulupirira Ine, ntchito zimene ndichita Ine adzazichitanso iyeyu; ndipo adzachita zoposa izi; chifukwa ndipita Ine kwa Atate. Ndipo chimene chilichonse mukafunse m'dzina langa, ndidzachichita, kuti Atate akalemekezedwe mwa Mwana. Ngati mudzapempha kanthu m'dzina langa, ndidzachita. Ngati mukonda Ine, sungani malamulo anga. Ndipo Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe ina, kuti akhale ndi inu kunthawi yonse, ndiye Mzimu wa choonadi; amene dziko lapansi silingathe kumlandira, pakuti silimuona Iye, kapena kumzindikira Iye. Inu mumzindikira Iye; chifukwa akhala ndi inu nadzakhala mwa inu. Sindidzakusiyani inu mukhale ana amasiye; ndidza kwa inu. Katsala kanthawi, ndipo dziko lapansi silindionanso Ine; koma inu mundiona; popeza Ine ndili ndi moyo inunso mudzakhala ndi moyo. Tsiku lomwelo mudzazindikira kuti ndili Ine mwa Atate wanga, ndi inu mwa Ine, ndi Ine mwa inu. Iye wakukhala nao malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo Ine ndidzamkonda, ndipo ndidzadzionetsa ndekha kwa iye. Yudasi, si Iskariote, ananena ndi Iye, Ambuye, chachitika chiyani kuti muziti mudzionetsa nokha kwa ife, koma si kwa dziko lapansi? Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo. Wosandikonda Ine sasunga mau anga; ndipo mau amene mumva sali mau anga, koma a Atate wondituma Ine. Izi ndalankhula nanu, pakukhala ndi inu. Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m'dzina langa, Iyeyo adzaphunzitsa inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu. Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. Mtima wanu usavutike, kapena usachite mantha. Mwamva kuti Ine ndinanena kwa inu, Ndimuka, ndipo ndidza kwa inu. Mukadandikonda Ine, mukadakondwera kuti ndipita kwa Atate; pakuti Atate ali wamkulu ndi Ine. Ndipo tsopano ndakuuzani chisanachitike, kuti pamene chitachitika mukakhulupirire. Sindidzalankhulanso zambiri ndi inu, pakuti mkulu wa dziko lapansi adza; ndipo alibe kanthu mwa Ine; koma kuti dziko lapansi lizindikire kuti ndikonda Atate, ndi kuti ndichita monga momwe Atate wandilamula. Nyamukani, tizimuka kuchokera kuno. Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate wanga ndiye wam'munda. Nthambi iliyonse ya mwa Ine yosabala chipatso, aichotsa; ndi iliyonse yakubala chipatso, aisadza, kuti ikabale chipatso chochuluka. Mwakhala okonzeka tsopano inu chifukwa cha mau amene ndalankhula ndi inu. Khalani mwa Ine, ndi Ine mwa inu. Monga nthambi siingathe kubala chipatso pa yokha, ngati siikhala mwampesa; motere mulibe inunso ngati simukhala mwa Ine. Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi zake: wakukhala mwa Ine, ndi Ine mwa iye, ameneyo abala chipatso chambiri; pakuti kopanda Ine simungathe kuchita kanthu. Ngati wina sakhala mwa Ine, watayika kunja monga nthambi, nafota; ndipo azisonkhanitsa nazitaya kumoto, nazitentha. Ngati mukhala mwa Ine, ndi mau anga akhala mwa inu, pemphani chilichonse chimene muchifuna ndipo chidzachitika kwa inu. Mwa ichi alemekezedwa Atate wanga, kuti mubale chipatso chambiri; ndipo mudzakhala ophunzira anga. Monga momwe Atate wandikonda Ine, Inenso ndakonda inu; khalani m'chikondi changa. Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m'chikondi changa; monga Iye ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m'chikondi chake. Izi ndalankhula ndi inu, kuti chimwemwe changa chikhale mwa inu, ndi kuti chimwemwe chanu chidzale. Lamulo langa ndi ili, kuti mukondane wina ndi mnzake, monga ndakonda inu. Palibe munthu ali nacho chikondi choposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake. Muli abwenzi anga inu, ngati muzichita zimene ndikulamulani inu. Sinditchanso inu akapolo; chifukwa kapolo sadziwa chimene mbuye wake achita; koma ndatcha inu abwenzi; chifukwa zonse zimene ndazimva kwa Atate wanga ndakudziwitsani. Inu simunandisankha Ine, koma Ine ndinakusankhani inu, ndipo ndinakuikani, kuti mukamuke inu ndi kubala chipatso, ndi kuti chipatso chanu chikhale; kuti chimene chilichonse mukapempha Atate m'dzina langa akakupatseni inu. Zinthu izi ndilamula inu, kuti mukondane wina ndi mnzake. Ngati dziko lapansi lida inu, mudziwa kuti lidada Ine lisanayambe kuda inu. Mukadakhala a dziko lapansi, dziko lapansi likadakonda zake za lokha; koma popeza simuli a dziko lapansi, koma Ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi, chifukwa cha ichi likudani inu. Kumbukirani mau amene Ine ndinanena kwa inu, Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wake. Ngati anandilondalonda Ine, adzakulondalondani inunso; ngati anasunga mau anga, adzasunga anunso. Koma izi zonse adzakuchitirani chifukwa cha dzina langa, chifukwa sadziwa wondituma Ine. Sindikadadza ndi kulankhula nao sakadakhala nalo tchimo; koma tsopano alibe chowiringula pa machimo ao. Iye wondida Ine, adanso Atate wanga. Sindikadachita mwa iwo ntchito zosachita wina, sakadakhala nalo tchimo; koma tsopano anaona, nada Ine ndi Atate wanganso. Koma chitero, kuti mau olembedwa m'chilamulo chao akwaniridwe, kuti, Anandida Ine kopanda chifukwa. Koma pamene wafika Nkhoswe, amene Ine ndidzamtuma kwa inu kuchokera kwa Atate, ndiye Mzimu wa choonadi, amene atuluka kwa Atate, Iyeyu adzandichitira Ine umboni. Ndipo inunso muchita umboni, pakuti muli ndi Ine kuyambira chiyambi. Izi ndalankhula ndi inu kuti mungakhumudwitsidwe. Adzakutulutsani m'masunagoge, koma ikudza nthawi imene yense wakupha inu adzayesa kuti atumikira Mulungu. Ndipo izi adzachita, chifukwa sanadziwa Atate, kapena Ine. Koma zinthu izi ndalankhula ndi inu kuti ikadza nthawi yao, mukakumbukire kuti ndinakuuzani. Koma izi sindinanena kwa inu kuyambira pachiyambi, chifukwa ndinali pamodzi ndi inu. Koma tsopano ndimuka kwa Iye wondituma Ine; ndipo palibe wina mwa inu andifunsa Ine, Munka kuti? Koma chifukwa ndalankhula izi ndi inu chisoni chadzala mumtima mwanu. Koma ndinena Ine choonadi ndi inu; kuyenera kwa inu kuti ndichoke Ine; pakuti ngati sindichoka, Nkhosweyo sadzadza kwa inu; koma ngati ndipita ndidzamtuma Iye kwa inu. Ndipo atadza Iyeyo, adzatsutsa dziko lapansi za machimo, ndi za chilungamo, ndi za chiweruziro; za machimo, chifukwa sakhulupirira Ine; za chilungamo, chifukwa ndinka kwa Atate, ndipo simundionanso; za chiweruzo, chifukwa mkulu wa dziko ili lapansi waweruzidwa. Ndili nazo zambirinso zakunena kwa inu, koma simungathe kuzisenza tsopano lino. Koma atadza Iyeyo, Mzimu wa choonadi, adzatsogolera inu m'choonadi chonse; pakuti sadzalankhula za Iye mwini; koma zinthu zilizonse adzazimva, adzazilankhula; ndipo zinthu zilinkudza adzakulalikirani. Iyeyo adzalemekeza Ine; chifukwa adzatenga za mwa Ine, nadzalalikira kwa inu. Zinthu zilizonse Atate ali nazo ndi zanga; chifukwa chake ndinati, kuti atenga za mwa Ine, nadzalalikira kwa inu. Katsala kanthawi, ndipo simundionanso Ine, ndipo kanthawinso, ndipo mudzandiona Ine. Mwa ophunzira ake tsono anati wina ndi mnzake, Ichi nchiyani chimene anena ndi ife, Kanthawi ndipo simundiona; ndiponso kanthawi, ndipo mudzandiona; ndipo, chifukwa ndimuka kwa Atate? Chifukwa chake ananena. Ichi nchiyani chimene anena, Kanthawi? Sitidziwa chimene alankhula. Yesu anazindikira kuti analikufuna kumfunsa Iye, ndipo anati kwa iwo, Kodi mulikufunsana wina ndi mnzake za ichi, kuti ndinati, Kanthawi ndipo simundiona Ine, ndiponso kanthawi nimudzandiona Ine? Indetu, indetu, ndinena ndi inu, kuti mudzalira ndi kubuma maliro inu, koma dziko lapansi lidzakondwera; mudzachita chisoni inu, koma chisoni chanu chidzasandulika chimwemwe. Mkazi pamene akuti abale ali nacho chisoni, chifukwa yafika nthawi yake; koma pamene wabala mwana, sakumbukiranso kusaukako, chifukwa cha chimwemwe kuti wabadwa munthu kudziko lapansi. Ndipo inu tsono muli nacho chisoni tsopano lino, koma ndidzakuonaninso, ndipo mtima wanu udzakondwera, ndipo palibe wina adzachotsa kwa inu chimwemwe chanu. Ndipo tsiku limenelo simudzandifunsa kanthu. Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Ngati mudzapempha Atate kanthu, adzakupatsani inu m'dzina langa. Kufikira tsopano simunapempha kanthu m'dzina langa; pemphani, ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chikwaniridwe. Zinthu izi ndalankhula ndi inu m'mafanizo; ikudza nthawi imene sindidzalankhula ndi inu m'mafanizo, koma ndidzakulalikirani inu m'mafanizo, koma ndidzakulalikirani inu momveka za Atate. Tsiku limenelo mudzapempha m'dzina langa; ndipo sindinena kwa inu kuti Ine ndidzafunsira inu kwa Atate; pakuti Atate yekha akonda inu, chifukwa inu mwandikonda Ine, ndi kukhulupirira kuti Ine ndinatuluka kwa Atate. Ndinatuluka mwa Atate, ndipo ndadza kudziko lapansi: ndilisiyanso dziko lapansi, ndipo ndipita kwa Atate. Ophunzira ake ananena, Onani, tsopano mulankhula zomveka, ndipo mulibe kunena chiphiphiritso. Tsopano tidziwa kuti mudziwa zonse, ndipo mulibe kusowa kuti wina akafunse Inu; mwa ichi tikhulupirira kuti munatuluka kwa Mulungu. Yesu anayankha iwo, Kodi mukhulupirira tsopano? Onani ikudza nthawi, ndipo yafika, imene mudzabalalitsidwa, yense ku zake za yekha, ndipo mudzandisiya Ine pa ndekha. Ndipo sindikhala pa ndekha, chifukwa Atate ali pamodzi ndi Ine, Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalingonjetsa dziko lapansi Ine. Zinthu izi analankhula Yesu; ndipo m'mene anakweza maso ake Kumwamba, anati, Atate, yafika nthawi; lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanu akulemekezeni Inu; monga mwampatsa Iye ulamuliro pa thupi lililonse, kuti onse amene mwampatsa Iye, awapatse iwo moyo wosatha. Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Khristu amene munamtuma. Ine ndalemekeza Inu pa dziko lapansi, m'mene ndinatsiriza ntchito imene munandipatsa ndichite. Ndipo tsopano, Atate Inu, lemekezani Ine ndi Inu nokha ndi ulemerero umene ndinali nao ndi Inu lisanakhale dziko lapansi. Ndalionetsera dzina lanu kwa anthu amene mwandipatsa Ine m'dziko lapansi; anali anu, ndipo mwandipatsa Ine iwo; ndipo adasunga mau anu. Azindikira tsopano kuti zinthu zilizonse zimene mwandipatsa Ine zichokera kwa Inu; chifukwa mau amene munandipatsa Ine ndinapatsa iwo; ndipo analandira, nazindikira koona kuti ndinatuluka kwa Inu, ndipo anakhulupirira kuti Inu munandituma Ine. Ine ndiwapempherera iwo; sindipempherera dziko lapansi, koma iwo amene mwandipatsa Ine, chifukwa ali anu: ndipo zanga zonse zili zanu, ndi zanu zili zanga; ndipo ndilemekezedwa mwa iwo. Sindikhalanso m'dziko lapansi, koma iwo ali m'dziko lapansi, ndipo Ine ndidza kwa Inu. Atate Woyera, sungani awa m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine, kuti akhale mmodzi, monga Ife. Pamene ndinakhala nao, Ine ndinalikuwasunga iwo m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine; ndipo ndinawasunga, ndipo sanatayika mmodzi yense wa iwo, koma mwana wa chitayiko, kuti lembo likwaniridwe. Koma tsopano ndidza kwa Inu; ndipo izi ndilankhula m'dziko lapansi, kuti akhale nacho chimwemwe changa chokwaniridwa mwa iwo okha. Ine ndawapatsa iwo mau anu; ndipo dziko lapansi, linadana nao, chifukwa sakhala a dziko lapansi, monga Ine sindikhala wa dziko lapansi. Sindipempha kuti muwachotse iwo m'dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woipayo. Siali a dziko lapansi monga Ine sindili wa dziko lapansi. Patulani iwo m'choonadi; mau anu ndi choonadi. Monga momwe munandituma Ine kudziko lapansi, Inenso ndinatuma iwo kudziko lapansi. Ndipo chifukwa cha iwo Ine ndidzipatula ndekha kuti iwonso akhale opatulidwa m'choonadi. Koma sindipempherera iwo okha, komanso iwo akukhulupirira Ine chifukwa cha mau ao; kuti onse akakhale amodzi, monga Inu Atate mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, kuti iwonso akakhale mwa Ife: kuti dziko lapansi likakhulupirire kuti Inu munandituma Ine. Ndipo ulemerero umene mwandipatsa Ine ndapatsa iwo; kuti akhale amodzi, monga Ife tili mmodzi; Ine mwa iwo, ndi Inu mwa Ine, kuti akhale angwiro mwa mmodzi; kuti dziko lapansi lizindikire kuti Inu munandituma Ine, nimunawakonda iwo, monga momwe munakonda Ine. Atate, amene mwandipatsa Ine, ndifuna kuti, kumene ndili Ine, iwonso akhale pamodzi ndi Ine; kuti ayang'anire ulemerero wanga, umene mwandipatsa Ine; pakuti munandikonda Ine lisanakhazikike dziko lapansi. Atate wolungama, dziko lapansi silinadziwa Inu, koma Ine ndinadziwa Inu; ndipo iwo anazindikira kuti munandituma Ine; ndipo ndinazindikiritsa iwo dzina lanu, ndipo ndidzalizindikiritsa; kuti chikondi chimene munandikonda nacho chikhale mwa iwo, ndi Ine mwa iwo. M'mene Yesu adanena izi, anatuluka ndi ophunzira ake, kunka tsidya lija la mtsinje wa Kidroni, kumene kunali munda, umene analowamo Iye ndi ophunzira ake. Koma Yudasinso amene akampereka Iye, anadziwa malowa; chifukwa Yesu akamkako kawirikawiri ndi ophunzira ake. Pamenepo Yudasi, m'mene adatenga gulu la asilikali ndi anyamata, kwa ansembe aakulu ndi Afarisi, anadza komweko ndi nyali ndi miuni ndi zida. Pamenepo Yesu, podziwa zonse zilinkudza pa Iye, anatuluka, nati kwa iwo, Mufuna yani? Anayankha Iye, Yesu Mnazarayo. Yesu ananena nao, Ndine. Koma Yudasi yemwe, wompereka Iye, anaima nao pamodzi. Ndipo m'mene anati kwa iwo, Ndine, anabwerera m'mbuyo, nagwa pansi. Pamenepo anawafunsanso, Mufuna yani? Koma iwo anati, Yesu Mnazarayo. Yesu anayankha, Nati, Ndine; chifukwa chake ngati mufuna Ine, lekani awa amuke; kuti akwaniridwe mau amene ati, Mwa iwo amene mwandipatsa Ine, sindinataya mmodzi. Pamenepo Simoni Petro pokhala nalo lupanga, analisolola nakantha kapolo wa mkulu wa ansembe, namsenga khutu lake lamanja. Koma dzina lake la kapoloyo ndiye Malkusi. Pamenepo Yesu anati kwa Petro, Longa lupanga m'chimake chake; chikho chimene Atate wandipatsa Ine sindimwere ichi kodi? Ndipo khamulo ndi kapitao wamkulu, ndi anyamata a Ayuda anagwira Yesu nammanga Iye, nayamba kupita naye kwa Anasi; pakuti anali mpongozi wa Kayafa, amene anali mkulu wa ansembe chaka chomwecho. Koma Kayafa anali uja wakulangiza Ayuda, kuti kuyenera munthu mmodzi afere anthu. Koma Simoni Petro ndi wophunzira wina anatsata Yesu. Koma wophunzira ameneyo anali wodziwika kwa mkulu wa ansembe, nalowa pamodzi ndi Yesu, m'bwalo la mkulu wa ansembe; koma Petro anaima kukhomo kunja. Chifukwa chake wophunzira winayo amene anadziwika kwa mkulu wa ansembe, anatuluka nalankhula ndi wapakhomo, nalowetsa Petro. Pamenepo mdzakazi wapakhomoyo ananena kwa Petro, Kodi suli iwenso wa ophunzira a munthu uyu? Iyeyu ananena, Sindine. Koma akapolo anyamata analikuimirirako, atasonkha moto wamakala; pakuti kunali kuzizira; ndipo analikuotha moto; koma Petronso anali nao alikuimirira ndi kuotha moto. Ndipo mkulu wa ansembe anafunsa Yesu za ophunzira ake, ndi chiphunzitso chake. Yesu anayankha iye, Ine ndalankhula zomveka kwa dziko lapansi; ndinaphunzitsa Ine nthawi zonse m'sunagoge ndi m'Kachisi, kumene amasonkhana Ayuda onse; ndipo mobisika sindinalankhula kanthu. Undifunsiranji Ine? Funsa iwo amene adamva chimene ndinalankhula nao; taona, amenewo adziwa chimene ndinanena Ine. Koma m'mene Iye adanena izi, mmodzi wa anyamata akuimirirako anapanda Yesu khofu, ndi kuti, Kodi uyankha mkulu wa ansembe chomwecho? Yesu anayankha iye, Ngati ndalankhula choipa, chita umboni wa choipacho, koma ngati bwino, undipandiranji? Koma Anasi adamtumiza Iye womangidwa kwa Kayafa mkulu wa ansembe. Koma Simoni Petro analikuimirira ndi kuotha moto. Pomwepo anati kwa iye, Suli iwenso wa ophunzira ake kodi? Iyeyu anakana, nati, Sindine. Mmodzi wa akapolo a mkulu wa ansembe ndiye mbale wake uja amene Petro anamdula khutu, ananena, Ine sindinakuona iwe kodi m'munda pamodzi ndi Iye? Pamenepo Petro anakananso; ndipo pomwepo analira tambala. Pamenepo anamtenga Yesu kuchokera kwa Kayafa kupita ku Pretorio; koma munali mamawa; ndipo iwo sanalowa ku Pretorio, kuti angadetsedwe, koma kuti akadye Paska. Chifukwa chake Pilato anatulukira kunja kwa iwo, nati, Chifukwa chanji mwadza nacho cha munthu uyu? Anayankha nati kwa iye, Akadakhala wosachita zoipa uyu sitikadampereka Iye kwa inu. Ndipo Pilato anati kwa iwo, Mumtenge Iye inu, ndi kumweruza Iye monga mwa chilamulo chanu. Ayuda anati kwa iye, Tilibe ulamuliro wakupha munthu aliyense; kuti mau a Yesu akwaniridwe, amene ananena akuzindikiritsa imfa imene akuti adzafa nayo. Chifukwa chake Pilato analowanso m'Pretorio, naitana Yesu, nati kwa Iye, Iwe ndiwe mfumu ya Ayuda kodi? Yesu anayankha, Kodi munena ichi mwa inu nokha, kapena ena anakuuzani za Ine? Pilato anayankha, Ndili ine Myuda kodi? Mtundu wako ndi ansembe aakulu anakupereka kwa ine; wachita chiyani? Yesu anayankha, Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi; ufumu wanga ukadakhala wa dziko lino lapansi, anyamata anga akadalimbika nkhondo, kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda; koma tsopano ufumu wanga suli wochokera konkuno. Pamenepo Pilato anati kwa Iye, Nanga kodi ndiwe Mfumu? Yesu anayankha, Munena kuti ndine Mfumu. Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza kudziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi. Yense wakukhala mwa choonadi amva mau anga. Pilato ananena kwa Iye, Choonadi nchiyani? Ndipo pamene adanena ichi, anatulukiranso kwa Ayudawo, nanena nao, Ine sindipeza konse chifukwa mwa Iye. Koma muli nao makhalidwe, akuti ndimamasulira inu mmodzi pa Paska; kodi mufuna tsono kuti ndimasulire inu mfumu ya Ayuda? Pomwepo anafuulanso, nanena, Si uyu, koma Barabasi. Koma Barabasi anali wachifwamba. Pamenepo tsono Pilato anatenga Yesu, namkwapula. Ndipo asilikali, m'mene analuka korona waminga anamveka pamutu pake, namfunda Iye malaya achibakuwa; nadza kwa Iye, nanena, Tikuoneni, mfumu ya Ayuda! Nampanda khofu. Ndipo Pilato anatulukanso kunja, nanena nao, Taonani, ndidza naye kwa inu kunja kuti mudziwe kuti sindipeza mwa Iye chifukwa chilichonse. Pamenepo Yesu anatuluka kunja, atavala korona waminga, ndi malaya achibakuwa. Ndipo ananena nao, Taonani munthuyu! Ndipo pamene ansembe aakulu ndi anyamata anamuona Iye, anafuula nanena, Mpachikeni, mpachikeni. Pilato ananenana nao, Mtengeni Iye inu nimumpachike; pakuti ine sindipeza chifukwa mwa Iye. Ayuda anamyankha iye, Tili nacho chilamulo ife, ndipo monga mwa chilamulocho ayenera kufa, chifukwa anadziyesera Mwana wa Mulungu. Ndipo pamene Pilato anamva mau awa, anaopa koposa. Ndipo analowanso ku Pretorio, nanena kwa Yesu, Muchoka kuti? Koma Yesu sanamyankha kanthu. Chifukwa chake Pilato ananena kwa Iye, Simulankhula ndi ine kodi? Simudziwa kodi kuti ulamuliro ndili nao wakukumasulani, ndipo ndili nao ulamuliro wakukupachikani? Yesu anamyankha iye, Simukadakhala nao ulamuliro uliwonse pa Ine, ngati sukadapatsidwa kwa inu kuchokera Kumwamba; chifukwa cha ichi iye wondipereka Ine kwa inu ali nalo tchimo loposa. Pa ichi Pilato anafuna kumasula Iye; koma Ayuda anafuula, ndi kunena, Ngati mumasula ameneyo, simuli bwenzi la Kaisara; yense wodziyesera yekha mfumu atsutsana naye Kaisara. Pamenepo Pilato, m'mene adamva mau awa, anatuluka ndi Yesu, nakhala pansi pa mpando woweruzira kumalo dzina lake, Bwalo lamiyala, koma m'Chihebri, Gabata. Koma linali tsiku lokonza Paska; panali monga ora lachisanu ndi chimodzi. Ndipo ananena kwa Ayuda, Taonani, mfumu yanu! Pamenepo anafuula iwowa, Chotsani, Chotsani, mpachikeni Iye! Pilato ananena nao, Ndipachike mfumu yanu kodi? Ansembe aakulu anayankha, Tilibe mfumu koma Kaisara. Ndipo pamenepo anampereka Iye kwa iwo kuti ampachike. Pamenepo anatenga Yesu; ndipo anasenza mtanda yekha, natuluka kunka kumalo otchedwa Malo a Bade, amene atchedwa m'Chihebri, Gologota: kumene anampachika Iye; ndipo pamodzi ndi Iye awiri ena, chakuno ndi chauko, koma Yesu pakati. Koma Pilato analemba lembo, naliika pamtanda. Koma panalembedwa, YESU MNAZARAYO, MFUMU YA AYUDA. Ndipo lembo ilo analiwerenga ambiri a Ayuda; chifukwa malo amene Yesu anapachikidwapo anali pafupi pa mudziwo; ndipo linalembedwa m'Chihebri, ndi m'Chilatini, ndi m'Chigriki. Pamenepo ansembe aakulu a Ayuda, ananena kwa Pilato, Musalembe, Mfumu ya Ayuda; koma kuti Iyeyu anati, Ndili mfumu ya Ayuda. Pilato anayankha, Chimene ndalemba, ndalemba. Pamenepo asilikali, m'mene adapachika Yesu, anatenga zovala zake, anadula panai, natenga wina china, wina china, ndiponso malaya; koma malaya anaombedwa monsemo kuyambira pamwamba pake, analibe msoko. Chifukwa chake anati wina kwa mnzake, Tisang'ambe awa, koma tichite maere, awa akhale a yani; kuti lembo likwaniridwe limene linena, Anagawana zovala zanga mwa iwo okha, ndi pa malaya anga anachitira maere. Ndipo asilikali anachita izi. Koma pamtanda wa Yesu anaimirira amake, ndi mbale wa amake, Maria, mkazi wa Kleopa, ndi Maria wa Magadala. Pamenepo Yesu pakuona amake, ndi wophunzira amene anamkonda, alikuimirirako, ananena kwa amake, Mkazi, taonani, mwana wanu! Pamene ananena kwa wophunzirayo, Taona, amai wako. Ndipo kuyambira ora lomweli wophunzirayo ananka naye kwao. Chitapita ichi Yesu, podziwa kuti zonse zidatha pomwepo kuti lembo likwaniridwe, ananena, Ndimva ludzu. Kunaikidwako chotengera chodzala ndi vinyo wosasayo pa phesi la hisope, nachifikitsa kukamwa kwake. Pamene Yesu tsono adalandira vinyo wosasayo anati, Kwatha; ndipo anawerama mutu, napereka mzimu. Pomwepo Ayuda, popeza panali tsiku lokonzera, kuti mitembo ingatsale pamtanda tsiku la Sabata, pakuti tsiku lomwelo la Sabata linali lalikulu, anapempha Pilato kuti miyendo yao ithyoledwe, ndipo achotsedwe. Chifukwa chake anadza asilikali nathyola miyendo ya woyambayo, ndi ya winayo wopachikidwa pamodzi ndi Iye; koma pofika kwa Yesu, m'mene anamuona Iye, kuti wafa kale, sanathyola miyendo yake; koma mmodzi wa asilikali anamgwaza ndi nthungo m'nthiti yake, ndipo panatuluka pomwepo mwazi ndi madzi. Ndipo iye amene anaona, wachita umboni, ndi umboni wake uli woona; ndipo iyeyu adziwa kuti anena zoona, kuti inunso mukakhulupirire. Pakuti izi zinachitika, kuti lembo likwaniridwe, Fupa la Iye silidzathyoledwa. Ndipo linenanso lembo lina, Adzayang'ana pa Iye amene anampyoza. Chitatha ichi Yosefe wa ku Arimatea, ndiye wophunzira wa Yesu, koma mobisika, chifukwa cha kuopa Ayuda, anapempha Pilato kuti akachotse mtembo wa Yesu. Ndipo Pilato analola. Chifukwa chake anadza, nachotsa mtembo wake. Koma anadzanso Nikodemo, amene anadza kwa Iye usiku poyamba paja, alikutenga chisanganizo cha mure ndi aloe, monga miyeso zana. Pamenepo anatenga mtembo wa Yesu, nauzenenga ndi nsalu zabafuta pamodzi ndi zonunkhira, monga mwa maikidwe a maliro a Ayuda. Koma kunali munda kumalo kumene anapachikidwako, ndi m'mundamo munali manda atsopano m'mene sanaikidwamo munthu aliyense nthawi zonse. Pomwepo ndipo anaika Yesu, chifukwa cha tsiku lokonzera la Ayuda, pakuti mandawo anali pafupi. Koma tsiku loyamba la Sabata anadza Maria wa Magadala mamawa, kusanayambe kucha, kumanda, napenya mwala wochotsedwa kumanda. Pomwepo anathamanga nadza kwa Simoni Petro ndi kwa wophunzira wina amene Yesu anamkonda, nanena nao, Anachotsa Ambuye kumanda, ndipo sitidziwa kumene anamuika Iye. Anatuluka tsono Petro ndi wophunzira winayo, nalinkupita kumanda. Koma anathamanga onse awiri pamodzi; ndipo wophunzira winayo anathamanga naposa Petro, nayamba kufika kumanda; ndipo m'mene anawerama chosuzumira anaona nsalu zabafuta zitakhala, komatu sanalowamo. Pamenepo anadzanso Simoni Petro alikumtsata iye, nalowa m'manda; ndipo anaona nsalu zabafuta zitakhala, ndi mlezo, umene unali pamutu pake, wosakhala pamodzi ndi nsalu zabafuta, koma wopindika padera pamalo pena. Pamenepo tsono analowanso wophunzira winayo, amene anayamba kufika kumanda, ndipo anaona, nakhulupirira. Pakuti kufikira pomwepo sanadziwa lembo lakuti ayenera Iye kuuka kwa akufa. Chifukwa chake ophunzirawo anachokanso, kunka kwao. Koma Maria analikuima kumanda kunja, alikulira. Ndipo m'mene alikulira anawerama chisuzumirire kumanda; ndipo anaona angelo awiri atavala zoyera, alikukhala mmodzi kumutu, ndi wina kumiyendo, kumene mtembo wa Yesu udagona. Ndipo iwowa ananena kwa iye, Mkazi, uliranji? Ananena nao, Chifukwa anachotsa Ambuye wanga, ndipo sindidziwa kumene anamuika Iye. M'mene adanena izi, anacheuka m'mbuyo, naona Yesu ali chilili, ndipo sanadziwa kuti ndiye Yesu. Yesu ananena naye, Mkazi, uliranji? Ufuna yani? Iyeyu poyesa kuti ndiye wakumunda, ananena ndi Iye, Mbuye ngati mwamnyamula Iye, ndiuzeni kumene mwamuika Iye, ndipo ndidzamchotsa. Yesu ananena naye, Maria. Iyeyu m'mene anacheuka, ananena ndi Iye m'Chihebri, Raboni; chimene chinenedwa, Mphunzitsi. Yesu ananena naye, Usandikhudze, pakuti sinditha kukwera kwa Atate; koma pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, Ndikwera kunka kwa Atate wanga, ndi Mulungu wanu. Maria wa Magadala anapita, nalalikira kwa ophunzirawo, kuti, Ndaona Ambuye; ndi kuti ananena izi kwa iye. Pamenepo, pokhala madzulo, tsiku lomwelo, loyamba la Sabata, makomo ali chitsekere, kumene anakhala ophunzira, chifukwa cha kuopa Ayuda, Yesu anadza naimirira pakati pao, nanena nao, Mtendere ukhale ndi inu. Ndipo pamene adanena ichi, anaonetsa iwo manja ake ndi nthiti zake. Pamenepo ophunzira anakondwera pakuona Ambuye. Chifukwa chake Yesu anatinso kwa iwo, Mtendere ukhale ndi inu; monga Atate wandituma Ine, Inenso ndituma inu. Ndipo pamene anati ichi anawapumira, nanena nao, Landirani Mzimu Woyera. Zochimwa za anthu ali onse muwakhululukira, zikhululukidwa kwa iwo; za iwo amene muzigwiritsa, zagwiritsidwa. Koma Tomasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, wotchedwa Didimo, sanakhala nao pamodzi, pamene Yesu anadza. Chifukwa chake ophunzira ena ananena naye, Tamuona Ambuye. Koma iye anati kwa iwo, Ndikapanda kuona m'manja ake chizindikiro cha misomaliyo, ndi kuika chala changa m'chizindikiro cha misomaliyo, ndi kuika dzanja langa kunthiti yake; sindidzakhulupirira. Ndipo pakupita masiku asanu ndi atatu ophunzira ake analinso m'nyumbamo, ndi Tomasi pamodzi nao. Yesu anadza, makomo ali chitsekere, naimirira pakati, nati, Mtendere ukhale ndi inu. Pomwepo ananena kwa Tomasi, Bwera nacho chala chako kuno, nuone manja anga, ndipo bwera nalo dzanja lako, nuliike kunthiti yanga, ndipo usakhale wosakhulupirira, koma wokhulupirira. Tomasi anayankha nati kwa Iye, Ambuye wanga, ndi Mulungu wanga. Yesu ananena kwa iye, Chifukwa wandiona Ine, wakhulupirira; odala iwo akukhulupirira, angakhale sanaona. Ndipo zizindikiro zina zambiri Yesu anazichita pamaso pa ophunzira ake, zimene sizinalembedwa m'buku ili; koma zalembedwa izi kuti mukakhulupirire kuti Yesu ndiye Khristu Mwana wa Mulungu, ndi kuti pakukhulupirira mukhale nao moyo m'dzina lake. Zitapita izi Yesu anadzionetseranso kwa ophunzira ake kunyanja ya Tiberiasi. Koma anadzionetsera chotere. Anali pamodzi Simoni Petro, ndi Tomasi, wotchedwa Didimo, ndi Natanaele wa ku Kana wa ku Galileya, ndi ana a Zebedeo, ndi awiri ena a ophunzira ake. Simoni Petro ananena nao, Ndinka kukasodza. Ananena naye, Ifenso tipita nawe. Anatuluka, nalowa m'ngalawa; ndipo m'usiku muja sanagwira kanthu. Koma pakuyamba kucha, Yesu anaimirira pambali pa nyanja, komatu ophunzirawo sanadziwa kuti ndiye Yesu. Yesu ananena nao, Ananu, muli nako kanthu kakudya kodi? Anamyankha Iye, Iai. Koma anati kwa iwo, Ponyani khoka kumbali ya dzanja lamanja ya ngalawa, ndipo mudzapeza. Pamenepo anaponya, ndipo analibenso mphamvu yakulikoka chifukwa cha kuchuluka nsomba. Pamenepo wophunzira uja amene Yesu anamkonda ananena kwa Petro, Ndiye Ambuye. Simoni Petro pakumva kuti ndiye Ambuye, anadziveka malaya a pathupi, pakuti anali wamaliseche, nadziponya yekha m'nyanja. Koma ophunzira ena anadza m'kangalawa, pakuti sanali kutali ndi mtunda, koma monga mikono mazana awiri, nakoka khoka la nsombazo. Ndipo pamene anatulukira pamtunda, anapenya moto wamakala pomwepo, ndi kansomba kosanjikikako, ndi mkate. Yesu ananena nao, Tenganiko nsomba zimene mwazigwira tsopano. Chifukwa chake Simoni Petro anakwera m'ngalawa nakokera khoka kumtunda lodzala ndi nsomba zazikulu, zana limodzi, ndi makumi asanu ndi zitatu; ndipo zingakhale zinachuluka kotere, kokha silinang'ambika. Yesu ananena nao, Idzani mufisule. Koma palibe mmodzi wa ophunzira anatha kumfunsa Iye, Ndinu yani? Podziwa kuti ndiye Ambuye. Yesu anadza natenga mkate napatsa iwo, momwemonso nsomba. Imeneyo ndi nthawi yachitatu yakudzionetsera Yesu kwa ophunzira ake, m'mene atauka kwa akufa. Ndipo pamene atafisula Yesu ananena kwa Simoni Petro, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine koposa awa? Ananena ndi Iye, Inde, Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu. Ananena naye, Dyetsa anaankhosa anga. Ananena nayenso kachiwiri, Simoni mwana wa Yona, ukonda Ine kodi? Ananena ndi Iye, Inde, Ambuye; mudziwa kuti ndikukondani Inu. Ananena naye, Weta nkhosa zanga. Ananena naye kachitatu, Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda Ine? Petro anamva chisoni kuti anati kwa iye kachitatu, Kodi undikonda Ine? Ndipo anati kwa iye, Ambuye, mudziwa Inu zonse; muzindikira kuti ndikukondani Inu. Yesu ananena naye, Dyetsa nkhosa zanga. Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, pamene unali mnyamata unadzimangira wekha m'chuuno, ndipo unayenda kumene unafuna; koma pamene udzakalamba udzatulutsa manja ako, ndipo adzakumanga wina, nadzakunyamula kumene sufuna. Koma ichi ananena ndi kuzindikiritsa imfa imene adzalemekeza nayo Mulungu. Ndipo m'mene ananena ichi, anati kwa iye, Nditsate Ine. Petro, m'mene anacheuka, anapenya wophunzira amene Yesu anamkonda alikutsata, amenenso anatsamira pachifuwa pake pamgonero, nati, Ambuye, ndani iye wakupereka Inu? Pamenepo Petro pakumuona, ananena kwa Yesu, Ambuye, koma nanga uyu? Yesu ananena naye, Ngati ndifuna uyu akhale kufikira ndidza Ine, kuli chiyani ndi iwe? Unditsate Ine iwe. Chifukwa chake mau awa anatuluka kufikira kwa abale, kuti wophunzira uyu sadzafa. Koma Yesu sananena kwa iye kuti sadzafa; koma, Ngati ndifuna iye akhale kufikira ndidza, kuli chiyani ndi iwe? Yemweyu ndiye wophunzira wakuchita umboni za izi, ndipo analembera izi; ndipo tidziwa kuti umboni wake ndi woona. Koma palinso zina zambiri zimene Yesu anazichita, zoti zikadalembedwa zonse phee, ndilingalira kuti dziko lapansi silikadakhala nao malo a mabuku amene akadalembedwa. Amen. Taonani Teofilo inu, mau aja oyamba ndinakonza, za zonse Yesu anayamba kuzichita ndi kuziphunzitsa, kufikira tsiku lija anatengedwa kunka Kumwamba, atatha kulamula mwa Mzimu Woyera atumwi amene adawasankha; kwa iwonso anadzionetsera yekha wamoyo ndi zitsimikizo zambiri, zitatha zowawa zake, naonekera kwa iwo masiku makumi anai, ndi kunena zinthu za Ufumu wa Mulungu; ndipo posonkhana nao pamodzi, anawalamulira asachoke ku Yerusalemu, komatu alindire lonjezano la Atate, limene, anati, munalimva kwa Ine; pakuti Yohane anabatizadi ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera, asanapite masiku ambiri. Pamenepo iwowa, atasonkhana pamodzi, anamfunsa Iye, nanena, Ambuye, kodi nthawi yino mubwezera ufumu kwa Israele? Koma anati kwa iwo, Sikuli kwa inu kudziwa nthawi kapena nyengo, zimene Atate anaziika m'ulamuliro wake wa Iye yekha. Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m'Yerusalemu, ndi m'Yudeya lonse, ndi m'Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko. Ndipo m'mene adanena izi, ali chipenyerere iwo, ananyamulidwa; ndipo mtambo unamlandira Iye kumchotsa kumaso kwao. Ndipo pakukhala iwo chipenyerere kumwamba pomuka Iye, taonani, amuna awiri ovala zoyera anaimirira pambali pao; amenenso anati, Amuna a ku Galileya, muimiranji ndi kuyang'ana kumwamba? Yesu amene walandiridwa kunka Kumwamba kuchokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuona alinkupita Kumwamba. Pamenepo anabwera ku Yerusalemu kuchokera kuphiri lonenedwa la Azitona, limene liyandikana ndi Yerusalemu, loyendako tsiku la Sabata. Ndipo pamene adalowa, anakwera kuchipinda chapamwamba, kumene analikukhalako; ndiwo Petro ndi Yohane ndi Yakobo ndi Andrea, Filipo ndi Tomasi, Bartolomeo ndi Mateyu, Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Simoni Zelote, ndi Yudasi mwana wa Yakobo. Iwo onse analikukangalika m'kupemphera, pamodzi ndi akazi, ndi Maria, amake wa Yesu, ndi abale ake omwe. Ndipo m'masiku awa anaimirira Petro pakati pa abale, nati (gulu la anthu losonkhana pamalo pomwe ndilo ngati zana limodzi ndi makumi awiri), Amuna inu, abale, kunayenera kuti lemba likwanitsidwe, limene Mzimu Woyera anayamba kunena mwa m'kamwa mwa Davide za Yudasi, wokhala mtsogoleri wa iwo adagwira Yesu. Chifukwa anali wowerengedwa mwa ife, ndipo analandira gawo lake la utumiki uwu. (Uyutu tsono anadzitengera kadziko ndi mphotho ya chosalungama; ndipo anagwa chamutu, naphulika pakati, ndi matumbo ake onse anakhuthuka; ndipo chinadziwika ndi onse akukhala ku Yerusalemu; kotero kuti m'manenedwe ao kadzikoka kanatchedwa Akeledama, ndiko, kadziko ka mwazi.) Pakuti kwalembedwa m'buku la Masalmo, Pogonera pake pakhale bwinja, ndipo pasakhale munthu wogonapo; ndipo uyang'aniro wake autenge wina. Potero kuyenera kuti wina wa amunawo anatsatana nafe nthawi yonseyi Ambuye Yesu analowa natuluka mwa ife, kuyambira ubatizo wa Yohane, kufikira tsiku lija anatengedwa kunka Kumwamba kutisiya ife, mmodzi wa awa akhale mboni ya kuuka kwake pamodzi ndi ife. Ndipo anaimikapo awiri, Yosefe wotchedwa Barsabasi, amene anatchedwanso Yusto, ndi Matiasi. Ndipo anapemphera, nati, Inu, Ambuye, wozindikira mitima ya onse, sonyezani mwa awa awiri mmodziyo amene munamsankha, alowe malo a utumiki uwu ndi utumwi, kuchokera komwe Yudasi anapatukira, kuti apite kumalo a iye yekha. Ndipo anayesa maere pa iwo; ndipo anagwera Matiasi; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo. Ndipo pakufika tsiku la Pentekoste, anali onse pamodzi pa malo amodzi. Ndipo mwadzidzidzi anamveka mau ochokera Kumwamba ngati mkokomo wa mphepo yolimba, nadzaza nyumba yonse imene analikukhalamo. Ndipo anaonekera kwa iwo malilime ogawanikana, onga amoto; ndipo unakhala pa iwo onse wayekhawayekha. Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa. Koma anali m'Yerusalemu okhalako Ayuda, amuna opembedza, ochokera kumtundu uliwonse pansi pa thambo. Koma pochitika mau awa, unyinji wa anthu unasonkhana, nusokonezedwa, popeza yense anawamva alikulankhula m'chilankhulidwe chake cha iye yekha. Ndipo anadabwa onse, nazizwa, nanena, Taonani, awa onse alankhulawa sali Agalileya kodi? Ndipo nanga ife timva bwanji, yense m'chilankhulidwe chathu chimene tinabadwa nacho? Aparti ndi Amedi, ndi Aelamu, ndi iwo akukhala m'Mesopotamiya, m'Yudeya, ndiponso m'Kapadokiya, m'Ponto, ndi m'Asiya; m'Frijiya, ndiponso m'Pamfiliya, m'Ejipito, ndi mbali za Libiya wa ku Kirene, ndi alendo ochokera ku Roma, ndiwo Ayuda, ndiponso opinduka, Akrete, ndi Aarabu, tiwamva iwo alikulankhula m'malilime athu zazikulu za Mulungu. Ndipo anadabwa onse, nathedwa nzeru, nanena wina ndi mnzake, Kodi ichi nchiyani? Koma ena anawaseka, nanena kuti, Akhuta vinyo walero. Koma Petro, anaimirira pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo, nakweza mau ake, nanena kwa iwo, nati, Amuna inu Ayuda, ndi inu nonse akukhala kwanu m'Yerusalemu, ichi chizindikirike kwa inu, ndipo tcherani khutu mau anga. Pakuti awa sanaledzera monga muyesa inu; pakuti ndi ora lachitatu lokha la tsiku; komatu ichi ndi chimene chinanenedwa ndi mneneri Yowele, Ndipo kudzali m'masiku otsiriza, anena Mulungu, ndidzathira cha Mzimu wanga pa thupi lililonse, ndipo ana anu amuna, ndi akazi adzanenera, ndipo anyamata anu adzaona masomphenya, ndi akulu anu adzalota maloto; ndiponso pa akapolo anga ndi pa adzakazi anga m'masiku awa ndidzathira cha Mzimu wanga; ndipo adzanenera. Ndipo ndidzapatsa zodabwitsa m'thambo la kumwamba, ndi zizindikiro pa dziko lapansi; mwazi, ndi moto, ndi mpweya wa utsi; dzuwa lidzasanduka mdima, ndi mwezi udzasanduka mwazi, lisanadze tsiku la Ambuye, lalikulu ndi loonekera. Ndipo kudzali, kuti yense amene akaitana pa dzina la Ambuye adzapulumutsidwa. Amuna inu Aisraele, mverani mau awa: Yesu Mnazarayo, mwamuna wochokera kwa Mulungu, wosonyezedwa kwa inu ndi zimphamvu, ndi zozizwa, ndi zizindikiro, zimene Mulungu anazichita mwa Iye pakati pa inu monga mudziwa nokha; ameneyo, woperekedwa ndi uphungu woikidwa ndi kudziwiratu kwa Mulungu, inu mwampachika ndi kumupha ndi manja a anthu osaweruzika; yemweyo Mulungu anamuukitsa, atamasula zowawa za imfa, mwakuti sikunali kotheka kuti Iye agwidwe nayo. Pakuti Davide anena za Iye, Ndinaona Mbuye pamaso panga nthawi zonse; chifukwa ali pa dzanja langa lamanja, kuti ndingasinthike; mwa ichi unakondwera mtima wanga, ndipo linasangalala lilime langa; ndipo thupi langanso lidzakhala m'chiyembekezo. Pakuti simudzasiya moyo wanga ku dziko la akufa, kapena simudzapereka Woyera wanu aone chivunde, munandidziwitsa ine njira za moyo; mudzandidzaza ndi kukondwera pamaso panu. Amuna inu, abale, kuloleka kunena poyera posaopa kwa inu za kholo lija Davide, kuti adamwalira naikidwanso, ndipo manda ake ali ndi ife kufikira lero lino. Potero, pokhala mneneri iye, ndi kudziwa kuti ndi lumbiro anamlumbirira Mulungu, kuti mwa chipatso cha m'chuuno mwake adzakhazika wina pa mpando wachifumu wake; iye pakuona ichi kale, analankhula za kuuka kwa Khristu, kuti sanasiyidwa m'dziko la akufa, ndipo thupi lake silinaona chivunde. Yesu ameneyo, Mulungu anamuukitsa; za ichi tili mboni ife tonse. Potero, popeza anakwezedwa ndi dzanja lamanja la Mulungu, nalandira kwa Atate lonjezano la Mzimu Woyera, anatsanulira ichi, chimene inu mupenya nimumva. Pakuti Davide sanakwera Kumwamba ai; koma anena yekha, Ambuye anati kwa Mbuye wanga, khalani kudzanja lamanja langa, kufikira ndikaike adani ako chopondapo mapazi ako. Pamenepo lizindikiritse ndithu banja lililonse la Israele, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Khristu, Yesu amene inu munampachika. Koma pamene anamva ichi, analaswa mtima, natitu kwa Petro ndi atumwi enawo, Tidzachita chiyani, amuna inu, abale? Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m'dzina la Yesu Khristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera. Pakuti lonjezano lili kwa inu, ndi kwa ana anu, ndi kwa onse akutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaitana. Ndipo ndi mau ena ambiri anachita umboni, nawadandaulira iwo, nanena, Mudzipulumutse kwa mbadwo uno wokhotakhota. Pamenepo iwo amene analandira mau ake anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu. Ndipo anali chikhalire m'chiphunzitso cha atumwi ndi m'chiyanjano, m'kunyema mkate ndi mapemphero. Koma panadza mantha pa anthu onse; ndipo zozizwa ndi zizindikiro zambiri zinachitika ndi atumwi. Ndipo onse akukhulupirira anali pamodzi, nakhala nazo zonse zodyerana. Ndipo zimene anali nazo, ndi chuma chao, anazigulitsa, nazigawira kwa onse, monga momwe yense anasowera. Ndipo tsiku ndi tsiku anali chikhalire ndi mtima umodzi m'Kachisi, ndipo ananyema mkate kunyumba kwao, nalandira chakudya ndi msangalalo, ndi mtima woona; nalemekeza Mulungu, ndi kukhala nacho chisomo ndi anthu onse. Ndipo Ambuye anawaonjezera tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe. Koma Petro ndi Yohane analikukwera kunka ku Kachisi pa ora lakupembedza, ndilo lachisanu ndi chinai. Ndipo munthu wina wopunduka miyendo chibadwire ananyamulidwa, amene akamuika masiku onse pa khomo la Kachisi lotchedwa Lokongola, kuti apemphe zaulere kwa iwo akulowa m'Kachisi; ameneyo, pakuona Petro ndi Yohane akuti alowe m'Kachisi, anapempha alandire chaulere. Ndipo Petro, pompenyetsetsa iye pamodzi ndi Yohane, anati, Tiyang'ane ife. Ndipo iye anavomereza iwo, nalingirira kuti adzalandira kanthu. Koma Petro anati, Siliva ndi golide ndilibe; koma chimene ndili nacho, ichi ndikupatsa, M'dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, yenda. Ndipo anamgwira iye kudzanja lake lamanja, namnyamutsa; ndipo pomwepo mapazi ake ndi mfundo za kumapazi zinalimbikitsidwa. Ndipo anazunzuka, naimirira, nayenda; ndipo analowa pamodzi nao m'Kachisi, nayenda, nalumpha, nayamika Mulungu. Ndipo anthu onse anamuona iye, alikuyenda ndi kuyamika Mulungu; namzindikira iye, kuti ndiye amene anakhala pa Khomo Lokongola la Kachisi: ndipo anadzazidwa ndi kudabwa ndi kuzizwa pa ichi chidamgwera. Koma m'mene anagwira Petro ndi Yohane, anawathamangira pamodzi anthu onse kukhonde lotchedwa la Solomoni, alikudabwa ndithu. Koma m'mene Petro anachiona, anayankha kwa anthu, Amuna inu a Israele, muzizwa naye bwanji ameneyo? Kapena mutipenyetsetsa ife bwanji, monga ngati tamyendetsa iye ndi mphamvu ya ife eni, kapena ndi chipembedzo chathu? Mulungu wa Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu, analemekeza Mwana wake Yesu; amene inu munampereka ndi kumkaniza pa Pilato, poweruza iyeyu kummasula. Koma inu munakaniza Woyera ndi Wolungamayo, ndipo munapempha kuti munthu wambanda apatsidwe kwa inu, ndipo munamupha Mkulu wa moyo; amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa; za ichi ife tili mboni. Ndipo pa chikhulupiriro cha m'dzina lake dzina lakelo linalimbikitsa iye amene mumuona, nimumdziwa; ndipo chikhulupiriro chili mwa Iye chinampatsa kuchira konse kumeneku pamaso pa inu nonse. Ndipo tsopano, abale, ndidziwa kuti munachichita mosadziwa, monganso akulu anu. Koma zimene Mulungu analalikiratu m'kamwa mwa aneneri onse, kuti adzamva kuwawa Khristu, Iye anakwaniritsa chotero. Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zochokera kunkhope ya Ambuye; ndipo atume amene anaikidwa kwa inu, Khristu Yesu; amene thambo la kumwamba liyenera kumlandira kufikira nthawi zakukonzanso zinthu zonse, zimene Mulungu analankhula za izo m'kamwa mwa aneneri ake oyera chiyambire. Mosetu anati, Mbuye Mulungu adzaukitsira inu mneneri mwa abale anu, ngati ine; mudzamvera iye m'zinthu zilizonse akalankhule nanu. Ndipo kudzali, kuti wamoyo aliyense samvera mneneri ameneyu, adzasakazidwa konse mwa anthu. Koma angakhale aneneri onse kuyambira Samuele ndi akumtsatira, onse amene analankhula analalikira za masiku awa. Inu ndinu ana a aneneri, ndi a panganolo Mulungu anapangana ndi makolo anu ndi kunena kwa Abrahamu, Ndipo mu mbeu yako mafuko onse a dziko adzadalitsidwa. Kuyambira ndi inu, Mulungu, ataukitsa Mwana wake, anamtuma kukudalitsani inu, ndi kukubwezani yense ku zoipa zake. Koma m'mene analikulankhula ndi anthu, ansembe ndi mdindo wa ku Kachisi ndi Asaduki anadzako, ovutika mtima chifukwa anaphunzitsa anthuwo, nalalikira mwa Yesu kuuka kwa akufa. Ndipo anawathira manja, nawaika m'ndende kufikira m'mawa; pakuti mpa madzulo pamenepo. Koma ambiri a iwo amene adamva mau anakhulupirira; ndipo chiwerengero cha amuna chinali ngati zikwi zisanu. Koma panali m'mawa mwake, anasonkhana pamodzi m'Yerusalemu oweruza, ndi akulu, ndi alembi; ndi Anasi mkulu wa ansembe, ndi Kayafa, ndi Yohane, ndi Aleksandro, ndi onse amene anali a fuko la mkulu wa ansembe. Ndipo m'mene anawaimika pakati, anafunsa kuti, Ndi mphamvu yanji, kapena m'dzina lanji, mwachita ichi inu? Pamenepo Petro, wodzala ndi Mzimu Woyera anati kwa iwo, Oweruza a anthu inu, ndi akulu, ngati ife lero tiweruzidwa chifukwa cha ntchito yabwino ya pa munthu wodwala, ndi machiritsidwe ake, zindikirani inu nonse, ndi anthu onse a Israele, kuti m'dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, amene inu munampachika pamtanda, amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa, mwa Iyeyu munthuyu aimirirapo pamaso panu, wamoyo. Iye ndiye mwalawo woyesedwa wopanda pake ndi inu omanga nyumba, umene unayesedwa mutu wa pangodya. Ndipo palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo. Koma pakuona kulimbika mtima kwa Petro ndi Yohane, ndipo pozindikira kuti ndiwo anthu osaphunzira ndi opulukira, anazizwa ndipo anawazindikira, kuti adakhala pamodzi ndi Yesu. Ndipotu pakuona munthu wochiritsidwayo alikuimirira pamodzi nao, analibe kanthu kakunena kotsutsa. Koma pamene anawalamulira iwo achoke m'bwalo la akulu, ananena wina ndi mnzake, kuti, Tidzawachitira chiyani anthu awa? Pakutitu chaoneka kwa onse akukhala m'Yerusalemu kuti chizindikiro chozindikirika chachitidwa ndi iwo, ndipo sitingathe kukana. Komatu tiwaopse asalankhulenso m'dzina ili kwa munthu aliyense, kuti chisabukenso kwa anthu. Ndipo anawaitana, nawalamulira kuti asanene konse kapena kuphunzitsa m'dzina la Yesu. Koma Petro ndi Yohane anayankha nati kwa iwo, Weruzani, ngati nkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu; pakuti sitingathe ife kuleka kulankhula zimene tinaziona ndi kuzimva. Koma m'mene anawaopsanso anawamasula, osapeza kanthu kakuwalanga, chifukwa cha anthu; pakuti onse analemekeza Mulungu chifukwa cha chomwe chidachitika. Pakuti anali wa zaka zake zoposa makumi anai munthuyo, amene chizindikiro ichi chakumchiritsa chidachitidwa kwa iye. Ndipo m'mene anamasulidwa, anadza kwa anzao a iwo okha, nawauza zilizonse ansembe aakulu ndi akulu adanena nao. Ndipo m'mene adamva, anakweza mau kwa Mulungu ndi mtima umodzi, nati, Mfumu, Inu ndinu wolenga thambo la kumwamba ndi dziko, ndi nyanja, ndi zonse zili m'menemo; amene mwa Mzimu Woyera, pakamwa pa kholo lathu Davide mtumiki wanu, mudati, Amitundu anasokosera chifukwa chiyani? Nalingirira zopanda pake anthu? Anadzindandalitsa mafumu a dziko, ndipo oweruza anasonkhanidwa pamodzi, kutsutsana ndi Ambuye, ndi Khristu wake. Pakuti zoonadi anasonkhanidwa m'mudzi muno Herode, ndi Pontio Pilato yemwe pamodzi ndi amitundu ndi anthu a Israele kumchitira choipa Mwana wanu wopatulika Yesu amene munamdzoza; kuti achite zilizonse dzanja lanu ndi uphungu wanu zidaweruziratu zichitike. Ndipo tsopano Ambuye, penyani mau ao akuopsa, ndipo patsani kwa akapolo anu alankhule mau anu ndi kulimbika mtima konse, m'mene mutambasula dzanja lanu kukachiritsa; ndi kuti zizindikiro ndi zozizwa zichitidwe mwa dzina la Mwana wanu wopatulika Yesu. Ndipo m'mene adapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mau a Mulungu molimbika mtima. Ndipo unyinji wa iwo akukhulupirira anali wa mtima umodzi ndi moyo umodzi; ndipo sananena mmodzi kuti kanthu ka chuma anali nacho ndi kake ka iye yekha; koma anali nazo zonse zodyerana. Ndipo atumwi anachita umboni ndi mphamvu yaikulu za kuuka kwa Ambuye Yesu; ndipo panali chisomo chachikulu pa iwo onse. Pakuti mwa iwo munalibe wosowa; pakuti onse amene anali nayo minda, kapena nyumba, anazigulitsa nabwera nao malonda ake a izo adazigulitsa, nawaika pa mapazi a atumwi; ndipo anagawira yense monga kusowa kwake. Ndipo Yosefe, wotchedwa ndi atumwi Barnabasi (ndilo losandulika mwana wa chisangalalo), Mlevi, fuko lake la ku Kipro, pokhala nao munda, anaugulitsa, nabwera nazo ndalama zake, naziika pa mapazi a atumwi. Koma munthu wina dzina lake Ananiya pamodzi ndi Safira mkazi wake, anagulitsa chao, napatula pa mtengo wake, mkazi yemwe anadziwa, natenga chotsala, nachiika pa mapazi a atumwi. Koma Petro anati, Ananiya, Satana anadzaza mtima wako chifukwa ninji kudzanyenga Mzimu Woyera, ndi kupatula pa mtengo wake wa mundawo? Pamene unali nao, sunali wako kodi? Ndipo pamene unagulitsa sunali m'manja mwako kodi? Bwanji chinalowa ichi mumtima mwako? Sunanyenga anthu, komatu Mulungu. Koma Ananiya pakumva mau awa anagwa pansi namwalira: ndipo mantha akulu anagwera onse akumvawo. Ndipo ananyamuka anyamata, namkulunga, namnyamula, natuluka naye, namuika. Koma atapita monga maora atatu, ndipo mkazi wake, wosadziwa chidachitikacho, analowa. Ndipo Petro ananena naye, Undiuze, ngati munagulitsa mundawo pa mtengo wakuti. Ndipo ananena, Inde, wakuti. Koma Petro anati kwa iye, Munapangana pamodzi bwanji kuyesa Mzimu wa Ambuye? Taona, mapazi ao a iwo amene anaika mwamuna wako ali pakhomo, ndipo adzakunyamula kutuluka nawe. Ndipo anagwa pansi pomwepo pa mapazi ake, namwalira; ndipo analowa anyamatawo, nampeza iye wafa, ndipo anamnyamula kutuluka naye, namuika kwa mwamuna wake. Ndipo anadza mantha akulu pa Mpingo wonse, ndi pa onse akumva izi. Ndipo mwa manja a atumwi zizindikiro ndi zozizwa zambiri zinachitidwa pa anthu; ndipo anali onse ndi mtima umodzi m'khonde la Solomoni. Koma palibe mmodzi wa otsalawo analimba mtima kuphatikana nao; komatu anthu anawakuzitsa; ndipo makamaka anaonjezedwa kwa Ambuye okhulupirira ambiri, ndiwo amuna ndi akazi; kotero kuti ananyamulanso natuluka nao odwala kumakwalala, nawaika pamakama ndi pamphasa, kuti, popita Petro, ngakhale chithunzi chake chigwere wina wa iwo. Komanso unasonkhana pamodzi unyinji wa anthu ochokera kumidzi yozungulira Yerusalemu, alikutenga odwala, ndi ovutika ndi mizimu yonyansa; ndipo anachiritsidwa onsewa. Koma anauka mkulu wa ansembe ndi onse amene anali naye, ndiwo a chipatuko cha Asaduki, nadukidwa, nathira manja atumwi, nawaika m'ndende ya anthu wamba. Koma mngelo wa Ambuye anatsegula pakhomo pa ndende usiku, nawatulutsa, nati, Pitani, ndipo imirirani, nimulankhule m'Kachisi kwa anthu onse mau a Moyo umene. Ndipo atamva ichi, analowa m'Kachisi mbandakucha, naphunzitsa. Koma anadza mkulu wa ansembe ndi iwo amene anali naye, nasonkhanitsa a bwalo la akulu, ndi akulu onse a ana a Israele, natuma kundende atengedwe ajawo. Koma anyamata amene adafikako sanawapeza m'ndende, ndipo pobwera anafotokoza, nanena, Nyumba yandende tinapeza chitsekere, ndi alonda alikuimirira pamakomo; koma pamene tinatsegula sitinapezamo mmodzi yense. Koma m'mene anamva mau awa mdindo wa Kachisi ndi ansembe aakulu anathedwa nzeru ndi iwo aja, kuti ichi chidzatani. Ndipo anadza wina nawafotokozera, kuti, Taonani, amuna aja mudawaika m'ndende ali m'Kachisi, alikuimirira ndi kuphunzitsa anthu. Pamenepo anachoka mdindo pamodzi ndi anyamata; anadza nao, koma osawagwiritsa, pakuti anaopa anthu, angaponyedwe miyala. Ndipo m'mene adadza nao, anawaika pa bwalo la akulu. Ndipo anawafunsa mkulu wa ansembe, nanena, Tidakulamulirani chilamulire, musaphunzitsa kutchula dzina ili; ndipo taonani, mwadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu, ndipo mufuna kutidzetsera ife mwazi wa munthu uja. Ndipo anayankha Petro ndi atumwi, nati, Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu. Mulungu wa makolo athu anaukitsa Yesu, amene munamupha inu, ndi kumpachika pamtengo. Ameneyo Mulungu anamkweza ndi dzanja lake lamanja, akhale Mtsogoleri ndi Mpulumutsi, kuti apatse kwa Israele kulapa, ndi chikhululukiro cha machimo. Ndipo ife ndife mboni za zinthu izi; Mzimu Woyeranso, amene Mulungu anapatsa kwa iwo akumvera Iye. Koma m'mene anamva iwo analaswa mtima, nafuna kuwapha. Koma ananyamukapo wina pa bwalo la akulu, ndiye Mfarisi, dzina lake Gamaliele, mphunzitsi wa chilamulo, wochitidwa ulemu ndi anthu onse, nalamula kuti atumwiwo akhale kunja pang'ono. Ndipo anati kwa iwo, Amuna inu a Israele, kadzichenjerani nokha za anthu awa, chimene muti muwachitire. Pakuti asanafike masiku ano anauka Teudasi, nanena kuti ali kanthu iye mwini; amene anthu anaphatikana naye, chiwerengero chao ngati mazana anai; ndiye anaphedwa; ndi onse amene anamvera iye anamwazika, napita pachabe. Atapita ameneyo, anauka Yudasi wa ku Galileya, masiku a kulembedwa, nakopa anthu amtsate. Iyeyunso anaonongeka, ndi onse amene anamvera iye anabalalitsidwa. Ndipo tsopano ndinena ndi inu, Lekani anthu amenewa, nimuwalole akhale; pakuti ngati uphungu umene kapena ntchito iyi ichokera kwa anthu, idzapasuka; koma ngati ichokera kwa Mulungu simungathe kuwapasula; kuti kapena mungapezeke otsutsana ndi Mulungu. Ndipo anavomerezana ndi iye; ndipo m'mene adaitana atumwi, anawakwapula nawalamulira asalankhule kutchula dzina la Yesu, ndipo anawamasula. Pamenepo ndipo anapita kuchokera kubwalo la akulu, nakondwera kuti anayesedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzinalo. Ndipo masiku onse, m'Kachisi ndi m'nyumba, sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira Khristu Yesu. Koma masiku awo, pakuchulukitsa ophunzira, kunauka chidandaulo, Agriki kudandaula pa Ahebri, popeza amasiye ao anaiwalika pa chitumikiro cha tsiku ndi tsiku. Ndipo khumi ndi awiriwo anaitana unyinji wa ophunzira, nati, Sikuyenera kuti ife tisiye kulalikira mau a Mulungu ndi kutumikira podyerapo. Chifukwa chake, abale, yang'anani mwa inu amuna asanu ndi awiri a mbiri yabwino, odzala ndi Mzimu ndi nzeru, amene tikawaike asunge ntchito iyi. Koma ife tidzalimbika m'kupemphera, ndi kutumikira mau. Ndipo mau amene anakonda unyinji wonse; ndipo anasankha Stefano, ndiye munthu wodzala ndi chikhulupiriro ndi Mzimu Woyera, ndi Filipo, ndi Prokoro, ndi Nikanore ndi Timoni, ndi Parmenasi, ndi Nikolasi, ndiye wopinduka wa ku Antiokeya: amenewo anawaika pamaso pa atumwi; ndipo m'mene adapemphera, anaika manja pa iwo. Ndipo mau a Mulungu anakula; ndipo chiwerengero cha ophunzira chidachulukatu ku Yerusalemu; ndipo khamu lalikulu la ansembe linamvera chikhulupirirocho. Ndipo Stefano, wodzala ndi chisomo ndi mphamvu, anachita zozizwa ndi zizindikiro zazikulu mwa anthu. Koma anauka ena a iwo ochokera m'sunagoge wa Alibertino, ndi Akirene, ndi Aaleksandriya, ndi mwa iwo a ku Silisiya ndi ku Asiya, natsutsana ndi Stefano. Ndipo sanathe kuilaka nzeru ndi Mzimu amene analankhula naye. Pamenepo anafuna anthu akumpitira pansi, ndi kuti, Tidamumva iye alikunenera Mose ndi Mulungu mau amwano. Ndipo anautsa anthu, ndi akulu, ndi alembi, namfikira, namgwira iye, nadza naye kubwalo la akulu, naimika mboni zonama, zakunena, Munthu ameneyo saleka kunenera malo oyera amene, ndi chilamulo; pakuti tinamumva iye alikunena, kuti, Yesu Mnazarayo amene adzaononga malo ano, nadzasanduliza miyambo imene Mose anatipatsa. Ndipo anampenyetsetsa onse akukhala m'bwalo la akulu, naona nkhope yake ngati nkhope ya mngelo. Ndipo mkulu wa ansembe anati, Zitero izi kodi? Ndipo Stefano anati, Amuna inu, abale, ndi atate, tamverani. Mulungu wa ulemerero anaonekera kwa kholo lathu Abrahamu, pokhala iye m'Mesopotamiya, asanayambe kukhala m'Harani; nati kwa iye, Tuluka kudziko lako ndi kwa abale ako, ndipo tiye kudziko limene ndidzakusonyeza iwe. Pamenepo anatuluka m'dziko la Akaldeya namanga m'Harani: ndipo, kuchokera kumeneko, atamwalira atate wake, Mulungu anamsuntha alowe m'dziko lino, m'mene mukhalamo tsopano; ndipo sanampatsa cholowa chake m'menemo, ngakhale popondapo phazi lake iai; ndipo anamlonjezera iye kuti adzampatsa ili, likhale lake, ndi la mbeu yake yomtsatira, angakhale analibe mwana pamenepo. Koma Mulungu analankhula chotero, kuti mbeu yake idzakhala alendo m'dziko la eni, ndipo adzawachititsa ukapolo, nadzawachitira choipa, zaka mazana anai. Ndipo mtundu amene udzawayesa akapolo, ndidzauweruza Ine, anatero Mulungu; ndipo zitapita izi adzatuluka, nadzanditumikira Ine m'malo muno. Ndipo anampatsa iye chipangano cha mdulidwe; ndipo kotero Abrahamu anabala Isaki, namdula tsiku lachisanu ndi chitatu; ndi Isaki anabala Yakobo, ndi Yakobo anabala makolo akulu aja khumi ndi awiri. Ndipo makolo akuluwa podukidwa naye Yosefe, anamgulitsa amuke naye ku Ejipito; ndipo Mulungu anali naye, namlanditsa iye m'zisautso zake zonse, nampatsa chisomo ndi nzeru pamaso pa Farao mfumu ya ku Ejipito; ndipo anamuika iye kazembe wa pa Ejipito ndi pa nyumba yake yonse. Koma inadza njala pa Ejipito ndi Kanani lonse, ndi chisautso chachikulu; ndipo sanapeza chakudya makolo athu. Koma pakumva Yakobo kuti muli tirigu m'Ejipito, anatuma makolo athu ulendo woyamba. Ndipo pa ulendo wachiwiri Yosefe anazindikirika ndi abale ake; ndipo fuko la Yosefe linaonekera kwa Farao. Ndipo Yosefe anatumiza, naitana Yakobo atate wake, ndi a banja lake lonse, ndiwo anthu makumi asanu ndi awiri mphambu asanu. Ndipo Yakobo anatsikira ku Ejipito; ndipo anamwalira, iye ndi makolo athu; ndipo anawanyamula kupita nao ku Sekemu, nawaika m'manda amene Abrahamu adagula ndi mtengo wake wa ndalama kwa ana a Hamori m'Sekemu. Koma m'mene inayandikira nthawi ya lonjezo limene Mulungu adalonjezana ndi Abrahamu, anthuwo anakula nachuluka m'Ejipito, kufikira inauka mfumu ina pa Ejipito, imene siinamdziwa Yosefe. Imeneyo inachenjerera fuko lathu, niwachitira choipa makolo athu, niwatayitsa tiana tao, kuti tingakhale ndi moyo. Nyengo yomweyo anabadwa Mose, ndiye wokoma ndithu pamaso pa Mulungu; ndipo anamlera miyezi itatu m'nyumba ya atate wake: ndipo pakutayika iye, anamtola mwana wamkazi wa Farao, namlera akhale mwana wake. Ndipo Mose anaphunzira nzeru zonse za Aejipito; nali wamphamvu m'mau ake ndi m'ntchito zake. Koma pamene zaka zake zinafikira ngati makumi anai, kunalowa mumtima mwake kuzonda abale ake ana a Israele. Ndipo pakuona wina woti alikumchitira choipa, iye anamtchinjiriza, nambwezera chilango wozunzayo, nakantha Mwejipito. Ndipo anayesa kuti abale ake akazindikira kuti Mulungu alikuwapatsa chipulumutso mwa dzanja lake; koma sanazindikira. Ndipo m'mawa mwake anawaonekera alikulimbana ndeu, ndipo anati awateteze, ayanjanenso, nati, Amuna inu, muli abale; muchitirana choipa bwanji? Koma iye wakumchitira mnzake choipa anamkankha, nati, Wakuika iwe ndani mkulu ndi wotiweruzira? Kodi ufuna kundipha ine, monga muja unapha Mwejipito dzulo? Ndipo Mose anathawa pa mau awa, nakhala mlendo m'dziko la Midiyani; kumeneko anabala ana amuna awiri. Ndipo zitapita zaka makumi anai, anamuonekera mngelo m'chipululu cha Sinai, m'lawi la moto wa m'chitsamba. Koma Mose pakuona, anazizwa pa choonekacho; ndipo pakuyandikira iye kukaona, kunadza mau a Ambuye, akuti, Ine ndine Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, ndi wa Isaki, ndi wa Yakobo. Ndipo Mose ananthunthumira, osalimbika mtima kupenyetsako. Ndipo Ambuye anati kwa iye, Masula nsapato kumapazi ako; pakuti pa malo amene upondapo mpopatulika. Kuona ndaona choipidwa nacho anthu anga ali m'Ejipito, ndipo amva kubuula kwao; ndipo ndatsika kuwalanditsa; ndipo tsopano, tiye kuno, ndikutume ku Ejipito. Mose uyu amene anamkana, ndi kuti, Wakuika iwe ndani mkulu ndi woweruza? Ameneyo Mulungu anamtuma akhale mkulu, ndi mombolo, ndi dzanja la mngelo womuonekera pachitsamba. Ameneyo anawatsogolera, natuluka nao atachita zozizwa ndi zizindikiro m'Ejipito, ndi m'Nyanja Yofiira, ndi m'chipululu zaka makumi anai. Uyu ndi Mose uja adati kwa ana a Israele, Mulungu adzakuutsirani Mneneri wa mwa abale anu, monga ine. Uyu ndiye amene anali mu Mpingo m'chipululu pamodzi ndi mngelo wakulankhula naye m'phiri la Sinai, ndi makolo athu: amene analandira maneno amoyo akutipatsa ife; amene makolo athu sanafuna kumvera iye, koma anamkankha achoke, nabwerera m'mbuyo mumtima mwao ku Ejipito, nati ndi Aroni, Tipangireni milungu yotitsogolera ife; pakuti Mose uja, amene anatitulutsa m'Ejipito, sitidziwa chomwe chamgwera. Ndipo anapanga mwanawang'ombe masiku omwewo, nabwera nayo nsembe kwa fanolo, nasekerera ndi ntchito za manja ao. Koma Mulungu anatembenuka, nawapereka iwo atumikire gulu la kumwamba; monga kwalembedwa m'buku la aneneri, Kodi mwapereka kwa Ine nyama zophedwa ndi nsembe zaka makumi anai m'chipululu, nyumba ya Israele inu? Ndipo munatenga chihema cha Moleki, ndi nyenyezi ya mulungu Refani, zithunzizo mudazipanga kuzilambira; ndipo ndidzakutengani kunka nanu m'tsogolo mwake mwa Babiloni. Chihema cha umboni chinali ndi makolo athu m'chipululu, monga adalamula Iye wakulankhula ndi Mose, achipange ichi monga mwa chithunzicho adachiona. Chimenenso makolo athu akudza m'mbuyo, analowa nacho ndi Yoswa polandira iwo zao za amitundu, amene Mulungu anawaingitsa pamaso pa makolo athu, kufikira masiku a Davide; amene anapeza chisomo pamaso pa Mulungu, napempha kuti apeze mokhalamo Mulungu wa Yakobo. Koma Solomoni anammangira nyumba. Komatu Wamwambamwambayo sakhala m'nyumba zomangidwa ndi manja; monga mneneri anena, Thambo la kumwamba ndilo mpando wachifumu wanga, ndi dziko lapansi chopondapo mapazi anga. Mudzandimangira nyumba yotani, ati Ambuye, kapena malo a mpumulo wanga ndi otani? Silinapanga dzanja langa zinthu izi zonse kodi? Ouma khosi ndi osadulidwa mtima ndi makutu inu, mukaniza Mzimu Woyera nthawi zonse; monga anachita makolo anu, momwemo inu. Ndiye yani wa aneneri makolo anu sanamzunza? Ndipo anawapha iwo amene anaonetseratu za kudza kwake kwa Wolungamayo; wa Iye amene mwakhala tsopano akumpereka ndi akumupha; inu amene munalandira chilamulo monga chidaikidwa ndi angelo, ndipo simunachisunga. Koma pakumva izi analaswa mtima, namkukutira mano. Koma iye, pokhala wodzala ndi Mzimu Woyera, anapenyetsetsa Kumwamba, naona ulemerero wa Mulungu, ndi Yesu alikuimirira pa dzanja lamanja la Mulungu, nati, Taonani, ndipenya m'Mwamba motseguka, ndi Mwana wa Munthu alikuimirira pa dzanja lamanja la Mulungu. Koma anafuula ndi mau akulu, natseka m'makutu mwao, namgumukira iye ndi mtima umodzi; ndipo anamtaya kunja kwa mudzi, namponya miyala; ndipo mbonizo zinaika zovala zao pa mapazi a mnyamata dzina lake Saulo. Ndipo anamponya miyala Stefano, alikuitana Ambuye, ndi kunena, Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga. Ndipo m'mene anagwada pansi, anafuula ndi mau akulu, Ambuye, musawaikire iwo tchimo ili. Ndipo m'mene adanena ichi, anagona tulo. Ndipo Saulo analikuvomerezana nao pa imfa yake. Ndipo tsikulo kunayamba kuzunza kwakukulu pa Mpingo unali m'Yerusalemu; ndipo anabalalitsidwa onse m'maiko a Yudeya ndi Samariya, koma osati atumwi ai. Ndipo anamuika Stefano anthu opembedza, namlira maliro akulu. Ndipo Saulo anapasula Mpingo, nalowa nyumba ndi nyumba, nakokamo amuna ndi akazi, nawaika m'ndende. Pamenepo ndipo iwo akubalalitsidwa anapitapita nalalikira mauwo. Ndipo Filipo anatsikira kumudzi wa ku Samariya, nawalalikira iwo Khristu. Ndipo makamuwo ndi mtima umodzi anasamalira zonenedwa ndi Filipo, pamene anamva, napenya zizindikiro zimene anazichita. Pakuti ambiri a iwo akukhala nayo mizimu yonyansa inawatulukira, yofuula ndi mau akulu; ndipo ambiri amanjenje, ndi opunduka, anachiritsidwa. Ndipo panakhala chimwemwe chachikulu m'mudzimo. Koma panali munthu dzina lake Simoni amene adachita matsenga m'mudzimo kale, nadabwitsa anthu a Samariya, ndi kunena kuti iye yekha ndiye munthu wamkulu; ameneyo anamsamalira onsewo, kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu, ndi kunena, Uyu ndiye mphamvu ya Mulungu, yonenedwa Yaikulu. Ndipo anamsamalira iye, popeza nthawi yaikulu adawadabwitsa iwo ndi matsenga ake. Koma pamene anakhulupirira Filipo wakulalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi dzina la Yesu Khristu, anabatizidwa, amuna ndi akazi. Ndipo Simoni mwini wake anakhulupiriranso: ndipo m'mene anabatizidwa, anakhalira ndi Filipo; ndipo pakuona zizindikiro ndi mphamvu zazikulu zilikuchitika, anadabwa. Koma pamene atumwi a ku Yerusalemu anamva kuti Samariya adalandira mau a Mulungu, anawatumizira Petro ndi Yohane; amenewo, m'mene adatsikirako, anawapempherera, kuti alandire Mzimu Woyera: pakuti kufikira pamenepo nkuti asanagwe pa wina mmodzi wa iwo; koma anangobatizidwa m'dzina la Ambuye Yesu. Pamenepo anaika manja pa iwo, ndipo analandira Mzimu Woyera. Koma pakuona Simoni kuti mwa kuika manja a atumwi anapatsidwa Mzimu Woyera, anawatengera ndalama, nanena, Ndipatseni inenso ulamuliro umene, kuti amene aliyense ndikaika manja pa iye, alandire Mzimu Woyera. Koma Petro anati kwa iye, Ndalama yako itayike nawe, chifukwa unalingirira kulandira mphatso ya Mulungu ndi ndalama. Ulibe gawo kapena cholandira ndi mau awa; pakuti mtima wako suli wolunjika pamaso pa Mulungu. Chifukwa chake lapa choipa chako ichi, pemphera Ambuye, kuti kapena akukhululukire iwe cholingirira cha mtima wako. Pakuti ndiona kuti wagwidwa ndi ndulu yowawa ndi nsinga ya chosalungama. Ndipo Simoni anayankha nati, Mundipempherere ine kwa Ambuye kuti zisandigwere izi mwanenazi. Pamenepo iwo, atatha kuchita umboni ndi kulankhula mau a Ambuye, anabwera kunka ku Yerusalemu, nalalikira Uthenga Wabwino kumidzi yambiri ya Asamariya. Koma mngelo wa Ambuye analankhula ndi Filipo, nanena, Nyamuka, nupite mbali ya kumwera, kutsata njira yotsika kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Gaza; ndiyo ya chipululu. Ndipo ananyamuka napita; ndipo taona munthu wa ku Etiopiya, mdindo wamphamvu wa Kandake, mfumu yaikazi ya Aetiopiya, ndiye wakusunga chuma chake chonse, amene anadza ku Yerusalemu kudzapemphera; ndipo analinkubwerera, nalikukhala pa galeta wake, nawerenga mneneri Yesaya. Ndipo Mzimu anati kwa Filipo, Yandikira, nudziphatike kugaleta uyu. Ndipo Filipo anamthamangira, namva iye alikuwerenga Yesaya mneneri, ndipo anati, Kodi muzindikira chimene muwerenga? Koma anati, Ndingathe bwanji, popanda munthu wonditsogolera ine? Ndipo anapempha Filipo akwere nakhale naye. Koma palembo pamene analikuwerengapo ndipo: Ngati nkhosa anatengedwa kukaphedwa, ndi monga mwanawankhosa ali duu pamaso pa womsenga, kotero sanatsegula pakamwa pake. M'kuchepetsedwa kwake chiweruzo chake chinachotsedwa; mbadwo wake adzaubukitsa ndani? Chifukwa wachotsedwa kudziko moyo wake. Ndipo mdindoyo anayankha Filipo, nati, Ndikupempha, mneneri anena ichi za yani? Za yekha, kapena za wina? Ndipo Filipo anatsegula pakamwa pake, nayamba pa lembo ili, nalalikira kwa iye Yesu. Ndipo monga anapita panjira pao, anadza kumadzi akuti; ndipo mdindoyo anati, Taonapo madzi; chindiletsa ine chiyani ndisabatizidwe? *** Ndipo anamuuza kuti aimitse galeta; ndipo anatsikira onse awiri kumadzi, Filipo ndi mdindoyo; ndipo anambatiza iye. Ndipo pamene anakwera kutuluka m'madzi, Mzimu wa Ambuye anakwatula Filipo; ndipo mdindo sanamuonanso, pakuti anapita njira yake wokondwera. Koma Filipo anapezedwa ku Azoto; ndipo popitapita analalikira Uthenga Wabwino m'midzi yonse, kufikira anadza iye ku Kesareya. Koma Saulo, wosaleka kupumira pa ophunzira a Ambuye kuopsa ndi kupha, ananka kwa mkulu wa ansembe, napempha kwa iye akalata akunka nao ku Damasiko ku masunagoge, kuti akapeza ena otsata Njirayo, amuna ndi akazi, akawatenge kudza nao omangidwa ku Yerusalemu. Ndipo poyenda ulendo wake, kunali kuti iye anayandikira Damasiko: ndipo mwadzidzidzi kudawala momzingira kuunika kochokera kumwamba; ndipo anagwa pansi, namva mau akunena naye, Saulo, Saulo, Undilondalonderanji? Koma anati, Ndinu yani Mbuye? Ndipo anati, Ndine Yesu amene umlondalonda; komatu, uka, nulowe m'mudzi, ndipo kudzanenedwa kwa iwe chimene uyenera kuchita. Ndipo amunawo akumperekeza iye anaima duu, atamvadi mau, koma osaona munthu. Ndipo Saulo anauka; koma potseguka maso ake, sanapenya kanthu; ndipo anamgwira dzanja, namtenga nalowa naye m'Damasiko. Ndipo anakhala masiku atatu wosaona, ndipo sanadya kapena kumwa. Koma ku Damasiko kunali wophunzira wina dzina lake Ananiya; ndipo Ambuye anati kwa iye m'masomphenya, Ananiya. Ndipo anati, Ndili pano, Ambuye, Ndipo Ambuye anati kwa iye, Tauka, pita ku khwalala lotchedwa Lolunjika, ndipo m'nyumba ya Yudasi ufunse za munthu dzina lake Saulo, wa ku Tariso: pakuti taona, alikupemphera ndipo anaona mwamuna dzina lake Ananiya, alikulowa, namuika manja, kuti apenyenso. Ndipo Ananiya anayankha nati, Ambuye, ndamva ndi ambiri za munthu uyu, kuti anachitiradi choipa oyera mtima anu m'Yerusalemu; ndi kuti pano ali nao ulamuliro wa kwa ansembe aakulu wakumanga onse akuitana pa dzina lanu. Koma Ambuye anati kwa iye, Pita; pakuti iye ndiye chotengera changa chosankhika, chakunyamula dzina langa pamaso pa amitundu ndi mafumu ndi ana a Israele; pakuti Ine ndidzamuonetsa iye zinthu zambiri ayenera iye kuzimva kuwawa chifukwa cha dzina langa. Ndipo anachoka Ananiya, nalowa m'nyumbayo; ndipo anaika manja ake pa iye, nati, Saulo, mbale, Ambuye wandituma ine, ndiye Yesu amene anakuonekerani pa njira wadzerayo, kuti upenyenso, ndi kudzazidwa ndi Mzimu Woyera. Ndipo pomwepo padagwa kuchoka m'maso mwake ngati mamba, ndipo anapenyanso; ndipo ananyamuka nabatizidwa; ndipo analandira chakudya, naona nacho mphamvu. Ndipo anakhala pamodzi ndi ophunzira a ku Damasiko masiku ena. Ndipo pomwepo m'masunagoge analalikira Yesu, kuti Iye ndiye Mwana wa Mulungu. Ndipo onse amene anamva anadabwa, nanena, Suyu iye amene anaononga m'Yerusalemu onse akuitana pa dzina ili? Ndipo wadza kuno kudzatero, kuti amuke nao omangidwa kwa ansembe aakulu. Koma Saulo anakula makamaka mumphamvu, nadodometsa Ayuda akukhala m'Damasiko, nawatsimikizira kuti ameneyo ndi Khristu. Ndipo atapita masiku ambiri, Ayuda anapangana kuti amuphe iye; koma chiwembu chao chinadziwika ndi Saulo. Ndipo anadikiranso pazipata usana ndi usiku kuti amuphe; koma ophunzira ake anamtenga usiku, nampyoletsa palinga, namtsitsa mu dengu. Koma m'mene anafika ku Yerusalemu, anayesa kudziphatika kwa ophunzira; ndipo anamuopa iye onse, osakhulupirira kuti ali wophunzira. Koma Barnabasi anamtenga, napita naye kwa atumwi, nawafotokozera umo adaonera Ambuye m'njira, ndi kuti analankhula naye, ndi kuti m'Damasiko adanena molimbika mtima m'dzina la Yesu. Ndipo anali pamodzi nao, nalowa natuluka ku Yerusalemu, nanena molimbika mtima m'dzina la Ambuye; ndipotu analankhula natsutsana ndi Agriki; koma anayesayesa kumupha iye. Koma m'mene abale anachidziwa, anapita naye ku Kesareya, namtumiza achokeko kunka ku Tariso. Pamenepo ndipo Mpingo wa m'Yudeya lonse ndi Galileya ndi Samariya unali nao mtendere, nukhazikika; ndipo unayenda m'kuopa kwa Ambuye ndi m'chitonthozo cha Mzimu Woyera, nuchuluka. Koma kunali, pakupita Petro ponseponse, anatsikiranso kwa oyera mtima akukhala ku Lida. Ndipo anapeza kumeneko munthu dzina lake Eneya, amene anagonera pamphasa zaka zisanu ndi zitatu; amene anagwidwa manjenje. Ndipo Petro anati kwa iye, Eneya, Yesu Khristu akuchiritsa iwe; uka, yalula mphasa yako. Ndipo anauka pomwepo. Ndipo anamuona iye onse akukhala ku Lida ndi ku Saroni, natembenukira kwa Ambuye amenewa. Koma m'Yopa munali wophunzira dzina lake Tabita, ndilo kunena Dorika; mkazi ameneyo anadzala ndi ntchito zabwino ndi zachifundo zimene anazichita. Ndipo kunali m'masiku awa, kuti anadwala iye, namwalira; ndipo atamsambitsa iye anamgoneka m'chipinda chapamwamba. Ndipo popeza Lida ndi pafupi pa Yopa, m'mene anamva ophunzirawo kuti Petro anali pomwepo, anamtumizira anthu awiri, namdandaulira, Musachedwa mudze kwa ife. Ndipo Petro ananyamuka, napita nao. M'mene anafikako, anapita naye kuchipinda chapamwamba; ndipo amasiye onse anaimirirapo pali iye, nalira, namuonetsa malaya ndi zovala zimene Dorika adasoka, pamene anali nao pamodzi. Koma Petro anawatulutsa onse, nagwada pansi, napemphera; ndipo potembenukira kumtembo anati, Tabita, uka. Ndipo anatsegula maso ake; ndipo pakuona Petro, anakhala tsonga. Ndipo Petro anamgwira dzanja, namnyamutsa; ndipo m'mene adaitana oyera mtima ndi amasiye, anampereka iye wamoyo. Ndipo kudadziwika ku Yopa konse: ndipo ambiri anakhulupirira Ambuye. Ndipo kunali, kuti anakhala iye m'Yopa masiku ambiri ndi munthu Simoni wofufuta zikopa. Ndipo kunali munthu ku Kesareya, dzina lake Kornelio, kenturiyo wa gulu lotchedwa la Italiya, ndiye munthu wopembedza, ndi wakuopa Mulungu ndi banja lake lonse, amene anapatsa anthu zachifundo zambiri, napemphera Mulungu kosaleka. Iye anapenya m'masomphenya poyera, mngelo wa Mulungu alinkudza kwa iye, ngati ora lachisanu ndi chinai la usana, nanena naye, Kornelio. Ndipo pompenyetsetsa iye ndi kuopa, anati, Nchiyani, Mbuye? Ndipo anati kwa iye, Mapemphero ako ndi zachifundo zako zinakwera zikhala chikumbutso pamaso pa Mulungu. Ndipo tsopano tumiza amuna ku Yopa, aitane munthu Simoni, wotchedwanso Petro; acherezedwa iye ndi wina Simoni wofufuta zikopa, nyumba yake ili m'mbali mwa nyanja. Ndipo m'mene atachoka mngelo amene adalankhula naye, anaitana anyamata ake awiri, ndi msilikali wopembedza, wa iwo amene amtumikira kosaleka; ndipo m'mene adawafotokozera zonse, anawatuma ku Yopa. Koma m'mawa mwake, pokhala paulendo pao iwowa, m'mene anayandikira mudzi, Petro anakwera pachindwi kukapemphera, ngati pa ora lachisanu ndi chimodzi; ndipo anagwidwa njala, nafuna kudya; koma m'mene analikumkonzera chakudya kudamgwera ngati kukomoka; ndipo anaona pathambo padatseguka, ndi chotengera chilinkutsika, chonga ngati chinsalu chachikulu, chogwiridwa pangodya zake zinai, ndi kutsikira padziko pansi; m'menemo munali nyama za miyendo inai za mitundu yonse, ndi zokwawa za padziko ndi mbalame za m'mlengalenga. Ndipo anamdzera mau, Tauka, Petro; ipha, mudye. Koma Petro anati, Iaitu, Mbuye; pakuti sindinadya ine ndi kale lonse kanthu wamba ndi konyansa. Ndipo mau anamdzeranso nthawi yachiwiri, Chimene Mulungu anayeretsa, usachiyesa chinthu wamba. Ndipo chinachitika katatu ichi; ndipo pomwepo chotengeracho chinatengedwa kunka kumwamba. Ndipo pokayikakayika Petro mwa yekha ndi kuti masomphenya adawaona akuti chiyani, taonani, amuna aja otumidwa ndi Kornelio, atafunsira nyumba ya Simoni, anaima pachipata, ndipo anaitana nafunsa ngati Simoni, wotchedwanso Petro, acherezedwako. Ndipo m'mene Petro analingirira za masomphenya, Mzimu anenana naye, Taona, amuna atatu akufuna iwe. Komatu tauka, nutsike, ndipo upite nao, wosakayikakayika; pakuti ndawatuma ndine. Ndipo Petro anatsikira kwa anthuwo, nati, Taonani, ine ndine amene mumfuna; chifukwa chake mwadzera nchiyani? Ndipo anati, Kornelio kenturiyoyo, munthu wolungama ndi wakuopa Mulungu, amene mtundu wonse wa Ayuda umchitira umboni, anachenjezedwa ndi mngelo woyera kuti atumize nakuitaneni mumuke kunyumba yake, ndi kumvetsa mau anu. Pamenepo anawalowetsa nawachereza. Ndipo m'mawa mwake ananyamuka natuluka nao, ndi ena a abale a ku Yopa anamperekeza iye. Ndipo m'mawa mwake analowa m'Kesareya. Koma Kornelio analikudikira iwo, atasonkhanitsa abale ake ndi mabwenzi ake enieni. Ndipo panali pakulowa Petro, Kornelio anakomana naye, nagwa pa mapazi ake, namlambira. Koma Petro anamuutsa iye, nanena, Nyamuka; inenso ndine munthu. Ndipo pakukamba naye, analowa, napeza ambiri atasonkhana; ndipo anati kwa iwo, Mudziwa inu nokha kuti sikuloledwa kwa munthu Myuda adziphatike kapena kudza kwa munthu wa mtundu wina; koma Mulungu anandionetsera ine ndisanenere aliyense ali munthu wamba kapena wonyansa; chifukwa chakenso ndinadza wosakana, m'mene munatuma kundiitana. Pamenepo ndifunsa, mwandiitaniranji? Ndipo Kornelio anati, Atapita masiku anai, kufikira monga ora ili, ndinalikupemphera m'nyumba yanga pa ora lachisanu ndi chinai; ndipo taonani, padaimirira pamaso panga munthu wovala chovala chonyezimira, nati Kornelio, lamveka pemphero lako, ndi zopereka zachifundo zako zakumbukika pamaso pa Mulungu. Chifukwa chake tumiza anthu ku Yopa, akaitane Simoni amene anenedwanso Petro; amene acherezedwa m'nyumba ya Simoni wofufuta zikopa, m'mbali mwa nyanja. Pamenepo ndinatumiza kwa inu osachedwa; ndipo mwachita bwino mwadza kuno. Chifukwa chake taonani tilitonse pano pamaso pa Mulungu, kumva zonse Ambuye anakulamulirani. Ndipo Petro anatsegula pakamwa pake, nati, Zoona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankho; koma m'mitundu yonse, wakumuopa Iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye. Mau amene anatumiza kwa ana a Israele, akulalikira Uthenga Wabwino wa mtendere mwa Yesu Khristu (ndiye Ambuye wa onse) mauwo muwadziwa inu, adadzawo ku Yudeya lonse, akuyamba ku Galileya, ndi ubatizo umene Yohane anaulalikira; za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye. Ndipo ife ndife mboni za zonse adazichita m'dziko la Ayuda ndi m'Yerusalemu; amenenso anamupha, nampachika pamtengo. Ameneyo, Mulungu anamuukitsa tsiku lachitatu, nalola kuti aonetsedwe, si kwa anthu onse ai, koma kwa mboni zosankhidwiratu ndi Mulungu, ndiwo ife amene tinadya ndi kumwa naye pamodzi, atauka iye kwa akufa. Ndipo anatilamulira ife tilalikire kwa anthu, ndipo tichite umboni kuti Uyu ndiye amene aikidwa ndi Mulungu akhale woweruza amoyo ndi akufa. Ameneyu aneneri onse amchitira umboni, kuti onse akumkhulupirira Iye adzalandira chikhululukiro cha machimo ao, mwa dzina lake. Petro ali chilankhulire, Mzimu Woyera anagwa pa onse akumva mauwo. Ndipo anadabwa okhulupirirawo akumdulidwe onse amene anadza ndi Petro, chifukwa pa amitundunso panathiridwa mphatso ya Mzimu Woyera. Pakuti anawamva iwo alikulankhula ndi malilime, ndi kumkuza Mulungu. Pamenepo Petro anayankha, Kodi pali munthu akhoza kuletsa madzi, kuti asabatizidwe awa, amene alandira Mzimu Woyera ngatinso ife? Ndipo analamulira iwo abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Pamenepo anampempha iye atsotse masiku. Koma atumwi ndi abale akukhala m'Yudeya anamva kuti amitundunso adalandira mau a Mulungu. Ndipo pamene Petro adakwera kudza ku Yerusalemu, iwo akumdulidwe anatsutsana naye, nanena kuti, Munalowa kwa anthu osadulidwa, ndi kudya nao. Koma Petro anayamba kuwafotokozera chilongosolere, nanena, Ndinali ine m'mudzi wa Yopa ndi kupemphera; ndipo m'kukomoka ndinaona masomphenya, chotengera chilikutsika, ngati chinsalu chachikulu chogwiridwa pangodya zake zinai; ndi kutsika kumwamba, ndipo chinadza pali ine; chimenecho ndidachipenyetsetsa ndinachilingirira, ndipo ndinaona nyama za miyendo inai za padziko ndi zilombo, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga. Ndipo ndinamvanso mau akunena ndi ine, Tauka Petro; ipha, nudye. Koma ndinati, Iaitu, Ambuye; pakuti kanthu wamba, kapena konyansa sikanalowe m'kamwa mwanga ndi kale lonse. Koma mau anayankha nthawi yachiwiri otuluka m'mwamba, Chimene Mulungu anachiyeretsa, usachiyesera chinthu wamba. Ndipo ichi chinachitika katatu; ndipo zinakwezekanso zonse kumwamba. Ndipo taonani, pomwepo amuna atatu anaima pa khomo la nyumba m'mene munali ife, anatumidwa kwa ine ochokera ku Kesareya. Ndipo Mzimu anandiuza ndinke nao, wosasiyanitsa konse. Ndipo abale awa asanu ndi mmodzi anandiperekezanso anamuka nane; ndipo tinalowa m'nyumba ya munthuyo; ndipo anatiuza ife kuti adaona mngelo wakuimirira m'nyumba yake, ndi kuti, Tumiza anthu ku Yopa, akaitane Simoni, wonenedwanso Petro; amene adzalankhula nawe mau, amene udzapulumutsidwa nao iwe ndi apabanja ako onse. Ndipo m'mene ndinayamba kulankhula, Mzimu Woyera anawagwera, monga anatero ndi ife poyamba paja. Ndipo ndinakumbuka mau a Ambuye, kuti ananena, Yohanetu anabatiza ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera. Ngati tsono Mulungu anawapatsa iwo mphatso yomweyi yonga ya kwa ife, pamene tinakhulupirira Ambuye Yesu Khristu, ndine yani kuti ndingathe kuletsa Mulungu? Ndipo pamene anamva izi, anakhala duu, nalemekeza Mulungu, ndi kunena, Potero Mulungu anapatsa kwa amitundunso kutembenukira mtima kumoyo. Pamenepo iwotu, akubalalika chifukwa cha chisautsocho chidadza pa Stefano, anafikira ku Fenisiya, ndi Kipro, ndi Antiokeya, osalankhula mau kwa wina yense koma kwa Ayuda okha. Koma panali ena mwa iwo, amuna a ku Kipro, ndi Kirene, amenewo, m'mene adafika ku Antiokeya, analankhula ndi Agriki, ndi kulalikira Uthenga Wabwino wa Ambuye Yesu. Ndipo dzanja la Ambuye linali nao; ndi unyinji wakukhulupirira unatembenukira kwa Ambuye. Ndipo mbiri yao inamveka m'makutu a Mpingo wakukhala m'Yerusalemu; ndipo anatuma Barnabasi apite kufikira ku Antiokeya; ameneyo, m'mene anafika, naona chisomo cha Mulungu, anakondwa; ndipo anawadandaulira onse, kuti atsimikize mtima kukhalabe ndi Ambuye; chifukwa anali munthu wabwino, ndi wodzala ndi Mzimu Woyera ndi chikhulupiriro: ndipo khamu lalikulu lidaonjezeka kwa Ambuye. Ndipo anatuluka kunka ku Tariso kufunafuna Saulo; ndipo m'mene anampeza, anadza naye ku Antiokeya. Ndipo kunali, kuti chaka chonse anasonkhana pamodzi mu Mpingo, naphunzitsa anthu aunyinji; ndipo ophunzira anayamba kutchedwa Akhristu ku Antiokeya. Koma masiku awa aneneri anatsika ku Yerusalemu kudza ku Antiokeya. Ndipo ananyamuka mmodzi wa iwo, dzina lake Agabu, nalosa mwa Mzimu, kuti padzakhala njala yaikulu pa dziko lonse lokhalamo anthu; ndiyo idadza masiku a Klaudio. Ndipo ophunzira, yense monga anakhoza, anatsimikiza mtima kutumiza zothandiza abale akukhala m'Yudeya; ichonso anachita, natumiza kwa akulu mwa dzanja la Barnabasi ndi Saulo. Koma nyengo imeneyo Herode mfumu anathira manja ena a m'Mpingo kuwachitira zoipa. Ndipo adapha ndi lupanga Yakobo mbale wa Yohane. Ndipo pakuona kuti kudakondweretsa Ayuda, anaonjezapo nagwiranso Petro. Ndipo awo ndi masiku a mkate wopanda chotupitsa. Ndipo m'mene adamgwira, anamuika m'ndende, nampereka kwa magulu anai a alonda, lonse anaianai, amdikire iye; ndipo anafuna kumtulutsa kudza naye kwa anthu atapita Paska. Pamenepo ndipo Petro anasungika m'ndende; koma Mpingo anampempherera iye kwa Mulungu kosalekeza. Ndipo pamene Herode anati amtulutse, usiku womwewo Petro analikugona pakati pa asilikali awiri, womangidwa ndi maunyolo awiri; ndipo alonda akukhala pakhomo anadikira ndende. Ndipo taonani, mngelo wa Ambuye anaimirirapo, ndipo kuunika kunawala mokhalamo iye; ndipo anakhoma Petro m'nthiti, namuutsa iye, nanena, Tauka msanga. Ndipo maunyolo anagwa kuchoka m'manja mwake. Ndipo mngelo anati kwa iye, Dzimangire m'chuuno, numange nsapato zako. Nachita chotero. Ndipo ananena naye, Funda chovala chako, nunditsate ine. Ndipo anatuluka, namtsata; ndipo sanadziwa kuti nchoona chochitidwa ndi mngelo, koma anayesa kuti alikuona masomphenya. Ndipo m'mene adapitirira podikira poyamba ndi pachiwiri, anadza kuchitseko chachitsulo chakuyang'ana kumudzi; chimene chidawatsegukira chokha; ndipo anatuluka, napitirira khwalala limodzi; ndipo pomwepo mngelo anamchokera. Ndipo Petro atatsitsimuka, anati, Tsopano ndidziwa zoona, kuti Ambuye anatuma mngelo wake nandilanditsa ine m'dzanja la Herode, ndi ku chilingiriro chonse cha Ayuda. Ndipo m'mene adalingirirapo, anadza kunyumba ya Maria amake wa Yohane wonenedwanso Marko; pamenepo ambiri adasonkhana pamodzi, ndipo analikupemphera. Ndipo m'mene anagogoda pa chitseko cha pakhomo, anadza kudzavomera mdzakazi, dzina lake Roda. Ndipo pozindikira mau ake a Petro, chifukwa cha kukondwera sanatsegula pakhomo, koma anathamanga nalowanso, nawauza kuti Petro alikuima pakhomo. Koma anati kwa iye, Wamisala iwe. Ndipo analimbika ndi kunena kuti nkutero. Ndipo ananena, Ndiye mngelo wake. Koma Petro anakhala chigogodere; ndipo m'mene adamtsegulira, anamuona iye, nadabwa. Koma m'mene adawatambasulira dzanja akhale chete, anawafotokozera umo adamtulutsira Ambuye m'ndende. Ndipo anati, Muwauze Yakobo ndi abale izi. Ndipo anatuluka napita kwina. Koma kutacha, panali phokoso lalikulu mwa asilikali, Petro wamuka kuti. Ndipo pamene Herode adamfunafuna, wosampeza, anafunsitsa odikira nalamulira aphedwe. Ndipo anatsika ku Yudeya kunka ku Kesareya, nakhalabe kumeneko. Koma Herode anaipidwa nao a ku Tiro ndi Sidoni; ndipo anamdzera iye ndi mtima umodzi, ndipo m'mene adakopa Blasito mdindo wa mfumu, anapempha mtendere, popeza dziko lao linapeza zakudya zochokera ku dziko la mfumu. Ndipo tsiku lopangira Herode anavala zovala zachifumu, nakhala pa mpando wachifumu, nawafotokozera iwo mau a pabwalo. Ndipo anthu osonkhanidwawo anafuula, Ndiwo mau a Mulungu, si a munthu ai. Ndipo pomwepo mngelo wa Ambuye anamkantha, chifukwa sanampatsa Mulungu ulemerero; ndipo anadyedwa ndi mphutsi, natsirizika. Koma mau a Mulungu anakula, nachulukitsa. Ndipo Barnabasi ndi Saulo anabwera kuchokera ku Yerusalemu m'mene adatsiriza utumiki wao, natenga Yohane wonenedwanso Marko amuke nao. Ndipo kunali aneneri ndi aphunzitsi ku Antiokeya mu Mpingo wa komweko, ndiwo Barnabasi, ndi Simeoni, wonenedwa Wakuda, ndi Lusio wa ku Kirene, Manaene woleredwa pamodzi ndi Herode chiwangacho, ndi Saulo. Ndipo pa kutumikira Ambuye iwowa, ndi kusala chakudya, Mzimu Woyera anati, Mundipatulire Ine Barnabasi ndi Saulo ku ntchito imene ndinawaitanirako. Pamenepo, m'mene adasala chakudya ndi kupemphera ndi kuika manja pa iwo, anawatumiza amuke. Pamenepo iwo, otumidwa ndi Mzimu Woyera, anatsikira ku Seleukiya; ndipo pochokerapo anapita m'ngalawa ku Kipro. Ndipo pokhala ku Salami, analalikira mau a Mulungu m'masunagoge a Ayuda; ndipo anali nayenso Yohane mnyamata wao. Ndipo m'mene anapitirira chisumbu chonse kufikira Pafosi, anapezapo munthu watsenga, mneneri wonyenga, ndiye Myuda, dzina lake Barayesu; ameneyo anali ndi kazembe Sergio Paulo, ndiye munthu wanzeru. Yemweyo anaitana Barnabasi ndi Saulo, nafunitsa kumva mau a Mulungu. Koma Elimasi watsengayo (pakuti dzina lake litero posandulika) anawakaniza, nayesa kupatutsa kazembe asakhulupirire. Koma Saulo, ndiye Paulo, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, anampenyetsetsa iye, nati, Wodzala ndi chinyengo chonse ndi chenjerero lonse, iwe, mwana wa mdierekezi, mdani wa chilungamo chonse, kodi sudzaleka kuipsa njira zolunjika za Ambuye? Ndipo tsopano, taona, dzanja la Ambuye lili pa iwe, ndipo udzakhala wakhungu wosapenya dzuwa nthawi. Ndipo pomwepo lidamgwera khungu ndi mdima; ndipo anamukamuka nafuna wina womgwira dzanja. Pamenepo kazembe, pakuona chochitikacho anakhulupirira, nadabwa nacho chiphunzitso cha Ambuye. Ndipo atamasula kuchokera ku Pafosi a ulendo wake wa Paulo anadza ku Perga wa ku Pamfiliya; koma Yohane anapatukana nao nabwerera kunka ku Yerusalemu. Koma iwowa, atapita pochokera ku Perga anafika ku Antiokeya wa m'Pisidiya; ndipo analowa m'sunagoge tsiku la Sabata, nakhala pansi. Ndipo m'mene adatha kuwerenga chilamulo ndi aneneri akulu a sunagoge anatuma wina kwa iwo, ndi kunena, Amuna inu, abale, ngati muli nao mau akudandaulira anthu, nenani. Ndipo Paulo ananyamuka, nakodola ndi dzanja, nati, Amuna a Israele, ndi inu akuopa Mulungu, mverani. Mulungu wa anthu awa Israele anasankha makolo athu, nakweza anthuwo pakugonerera iwo m'dziko la Ejipito, ndipo ndi dzanja lokwezeka anawatulutsa iwo m'menemo. Ndipo monga nthawi ya zaka makumi anai anawalekerera m'chipululu. Ndipo m'mene adaononga mitundu ya anthu isanu ndi iwiri m'Kanani, anawapatsa cholowa dziko lao, monga zaka mazana anai kudza makumi asanu; ndipo zitatha izi anawapatsa oweruza kufikira Samuele mneneriyo. Ndipo kuyambira pamenepo anapempha mfumu; ndipo Mulungu anawapatsa Saulo mwana wa Kisi, munthu wa fuko la Benjamini, zaka makumi anai. Ndipo m'mene atamchotsa iye, anawautsira Davide akhale mfumu yao; amenenso anamchitira umboni, nati, Ndapeza Davide, mwana wa Yese, munthu wa pamtima panga, amene adzachita chifuniro changa chonse. Wochokera mu mbeu yake Mulungu, monga mwa lonjezano, anautsira Israele Mpulumutsi, Yesu; Yohane atalalikiratu, asanafike Iye, ubatizo wa kulapa kwa anthu onse a Israele. Ndipo pakukwaniritsa njira yake Yohane, ananena, Muyesa kuti ine ndine yani? Ine sindine Iye. Koma taonani, akudza wina wonditsata ine, amene sindiyenera kummasulira nsapato za pa mapazi ake. Amuna, abale, ana a mbadwa ya Abrahamu, ndi iwo mwa inu akuopa Mulungu, kwa ife atumidwa mau a chipulumutso ichi. Pakuti iwo akukhala m'Yerusalemu, ndi akulu ao, popeza sanamzindikira Iye, ngakhale mau a aneneri owerengedwa masabata onse, anawakwaniritsa pakumtsutsa. Ndipo ngakhale sanapeza chifukwa cha kumphera, anapempha Pilato kuti aphedwe. Ndipo atatsiriza zonse zolembedwa za Iye, anamtsitsa kumtengo, namuika m'manda. Koma Mulungu anamuukitsa Iye kwa akufa; ndipo anaonekera masiku ambiri ndi iwo amene anamperekeza Iye pokwera ku Yerusalemu kuchokera ku Galileya, amenewo ndiwo akumchitira umboni tsopano kwa anthu. Ndipo ife tikulalikirani inu Uthenga Wabwino wa lonjezano lochitidwa kwa makolo; kuti Mulungu analikwaniritsa ili kwa ana athu pakuukitsa Yesu; monganso mulembedwa m'Salimo lachiwiri, Iwe ndiwe Mwana wanga, lero ndakubala. Ndipo kuti anamuukitsa Iye kwa akufa, wosabweranso kuchivundi, anateropo, Ndidzakupatsani inu madalitso oyera ndi okhulupirika a Davide. Chifukwa anenanso m'Salimo lina, Simudzapereka Woyera wanu aone chivundi. Pakutitu, Davide, m'mene adautumikira uphungu wa Mulungu m'mbadwo mwake mwa iye yekha, anagona tulo, naikidwa kwa makolo ake, naona chivundi; koma Iye amene Mulungu anamuukitsa sanaona chivundi. Potero padziwike ndi inu amuna abale, kuti mwa Iye chilalikidwa kwa inu chikhululukiro cha machimo; ndipo mwa Iye yense wokhulupirira ayesedwa wolungama kumchotsera zonse zimene simunangathe kudzichotsera poyesedwa wolungama ndi chilamulo cha Mose. Chifukwa chake penyerani, kuti chingadzere inu chonenedwa ndi aneneriwo: Taonani, opeputsa inu, zizwani, kanganukani; kuti ndigwiritsa ntchito Ine masiku anu, ntchito imene simudzaikhulupirira wina akakuuzani. Ndipo pakutuluka iwo anapempha kuti alankhule naonso mau awa Sabata likudzalo. Ndipo m'mene anthu a m'sunagoge anabalalika, Ayuda ambiri ndi akupinduka opembedza anatsata Paulo ndi Barnabasi; amene, polankhula nao, anawaumiriza akhale m'chisomo cha Mulungu. Ndipo Sabata linalo udasonkhana pamodzi ngati mudzi wonse kumva mau a Mulungu. Koma Ayuda, pakuona makamu a anthu, anadukidwa, natsutsana nazo zolankhulidwa ndi Paulo, nachita mwano. Ndipo Paulo ndi Barnabasi analimbika mtima ponena, nati, Kunafunika kuti mau a Mulungu ayambe alankhulidwe kwa inu. Popeza muwakankha, nimudziyesera nokha osayenera moyo wosatha, taonani, titembenukira kwa amitundu. Pakuti kotero anatilamula Ambuye ndi kuti, Ndakuika iwe kuunika kwa amitundu, kuti udzakhala iwe chipulumutso kufikira malekezero a dziko. Ndipo pakumva ichi amitundu anakondwera, nalemekeza mau a Mulungu; ndipo anakhulupirira onse amene anaikidwiratu kumoyo wosatha. Ndipo mau a Ambuye anabukitsidwa m'dziko lonse. Koma Ayuda anakakamiza akazi opembedza ndi omveka, ndi akulu a mudziwo, nawautsira chizunzo Paulo ndi Barnabasi, ndipo anawapirikitsa iwo m'malire ao. Koma iwo, m'mene adawasansira fumbi la ku mapazi ao anadza ku Ikonio. Ndipo ophunzira anadzazidwa ndi chimwemwe ndi Mzimu Woyera. Ndipo kunali pa Ikonio kuti analowa pamodzi m'sunagoge wa Ayuda, nalankhula kotero, kuti khamu lalikulu la Ayuda ndi Agriki anakhulupirira. Koma Ayuda osamvera anautsa mitima ya Agriki kuti aipse abale athu. Chifukwa chake anakhala nthawi yaikulu nanenetsa zolimba mtima mwa Ambuye, amene anachitira umboni mau a chisomo chake, napatsa zizindikiro ndi zozizwa kuti zichitidwe ndi manja ao. Ndipo khamu la mudziwo linagawikana; ena anali ndi Ayuda, koma ena anali ndi atumwi. Ndipo pamene panakhala chigumukiro cha Agriki ndi cha Ayuda ndi akulu ao, cha kuwachitira chipongwe ndi kuwaponya miyala, iwo anamva, nathawira kumidzi ya Likaoniya, Listara ndi Deribe, ndi dziko lozungulirapo: kumeneko ndiko Uthenga Wabwino. Ndipo pa Listara panakhala munthu wina wopanda mphamvu ya m'mapazi mwake, wopunduka chibadwire, amene sanayenda nthawi zonse. Ameneyo anamva Paulo alinkulankhula; ndipo Paulo pomyang'anitsa, ndi kuona kuti anali ndi chikhulupiriro cholandira nacho moyo, anati ndi mau akulu, Taimirira. Ndipo iyeyu anazunzuka, nayenda. Pamene makamu anaona chimene anachita Paulo, anakweza mau ao, nati m'chinenero cha Likaoniya, Milungu yatsikira kwa ife monga anthu. Ndipo anamutcha Barnabasi, Zeusi; ndi Paulo, Heremesi, chifukwa anali wotsogola kunena. Koma wansembe wa Zeusi wa kumaso kwa mudzi, anadza nazo ng'ombe ndi maluwa kuzipata, nafuna kupereka nsembe pamodzi ndi makamu. Pamene anamva atumwi Paulo ndi Barnabasi, anang'amba zofunda zao, natumphira m'khamu, nafuula nati, Anthuni, bwanji muchita zimenezi? Ifenso tili anthu a mkhalidwe wathu umodzimodzi ndi wanu, akulalikira kwa inu Uthenga Wabwino, wakuti musiye zinthu zachabe izi, nimutembenukire kwa Mulungu wamoyo, amene analenga zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zonse zili momwemo: m'mibadwo yakale Iye adaleka mitundu yonse iyende m'njira mwao. Koma sanadzisiyira Iye mwini wopanda umboni, popeza anachita zabwino, nakupatsani inu zochokera kumwamba mvula ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima yanu ndi chakudya ndi chikondwero. Pakunena izo, anavutika pakuletsa makamu kuti asapereke nsembe kwa iwo. Ndipo anafika kumeneko Ayuda kuchokera ku Antiokeya ndi Ikonio; nakopa makamu, ndipo anamponya Paulo miyala, namguzira kunja kwa mudzi; namuyesa kuti wafa. Koma pamene anamzinga ophunzirawo, anauka iye, nalowa m'mudzi; m'mawa mwake anatuluka ndi Barnabasi kunka ku Deribe. Pamene analalikira Uthenga Wabwino pamudzipo, nayesa ambiri ophunzira, anabwera ku Listara ndi Ikonio ndi Antiokeya, nalimbikitsa mitima ya ophunzira, nadandaulira iwo kuti akhalebe m'chikhulupiriro, ndi kuti tiyenera kulowa m'ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri. Ndipo pamene anawaikira akulu mosankha mu Mpingo uliwonse, ndi kupemphera pamodzi ndi kusala kudya, naikiza iwo kwa Ambuye amene anamkhulupirirayo. Ndipo anapitirira pa Pisidiya, nafika ku Pamfiliya. Ndipo atalankhula mau m'Perga, anatsikira ku Ataliya; komweko anachoka m'ngalawa kunka ku Antiokeya, kumene anaikizidwa ku chisomo cha Mulungu ku ntchito imene adaimalizayo. Pamene anafika nasonkhanitsa Mpingo anabwerezanso zomwe Mulungu anachita nao, kuti anatsegulira amitundu pa khomo la chikhulupiriro. Ndipo anakhala pamenepo ndi ophunzira nthawi yaikulu. Ndipo anadza ena akutsika ku Yudeya, nawaphunzitsa abale, nati, Mukapanda kudulidwa monga mwambo wa Mose, simungathe kupulumuka. Ndipo pamene Paulo ndi Barnabasi anachitana nao makani ndi mafunsano, abale anapatula Paulo ndi Barnabasi, ndi ena a iwo, kuti akwere kunka ku Yerusalemu kwa atumwi ndi akulu kukanena za funsolo. Ndipo iwo anaperekezedwa ndi Mpingo, napita pa Fenisiya ndi Samariya, nafotokozera chisanduliko cha amitundu; nakondweretsa kwambiri abale onse. Pamene anafika ku Yerusalemu, analandiridwa ndi Mpingo, ndi atumwi ndi akulu, ndipo anabwerezanso zonse zimene Mulungu anachita nao. Koma anauka ena a mpatuko wa Afarisi okhulupirira, nati, Kuyenera kuwadula iwo, ndi kuwauza kuti asunge chilamulo cha Mose. Ndipo anasonkhana atumwi ndi akulu kuti anene za mlanduwo. Ndipo pamene panali mafunsano ambiri, Petro anaimirira, nati kwa iwo, Abale, mudziwa kuti poyamba Mulungu anasankha mwa inu, kuti m'kamwa mwanga amitundu amve mau a Uthenga Wabwino, nakhulupirire. Ndipo Mulungu, amene adziwa mtima, anawachitira umboni; nawapatsa Mzimu Woyera, monga anatipatsa ife; ndipo sanalekanitsa ife ndi iwo, nayeretsa mitima yao m'chikhulupiriro. Nanga bwanji tsopano mulikumuyesa Mulungu, kuti muike pa khosi la ophunzira goli, limene sanatha kunyamula kapena makolo athu kapena ife? Koma tikhulupirira tidzapulumuka mwa chisomo cha Ambuye Yesu Khristu, monga iwo omwe. Ndipo khamu lonse linatonthola; ndipo anamvera Barnabasi ndi Paulo alikubwerezanso zizindikiro ndi zozizwitsa zimene Mulungu anachita nao pa amitundu. Pamene iwo anatonthola Yakobo anayankha, nati, Abale, mverani ine: Simoni wabwereza kuti poyamba Mulungu anayang'anira amitundu, kuti atenge mwa iwo anthu a dzina lake. Ndipo mau a aneneri avomereza pamenepo; monga kunalembedwa, Zikatha izo ndidzabwera, ndidzamanganso chihema cha Davide, chimene chinagwa; ndidzamanganso zopasuka zake, ndipo ndidzachiimikanso: Kuti anthu otsalira afunefune Ambuye, ndi amitundu onse amene dzina langa linatchulidwa pa iwo, ati Ambuye, amene azidziwitsa zinthu zonsezo chiyambire dziko lapansi. Chifukwa chake ine ndiweruza, kuti tisavute a mwa amitundu amene anatembenukira kwa Mulungu, koma kuti tilembere kwa iwo, kuti asale zonyansa za mafano, ndi dama, ndi zopotola, ndi mwazi. Pakuti Mose, kuyambira pa mibadwo yakale ali nao m'midzi yonse amene amlalikira, akuwerenga mau ake m'masunagoge masabata onse. Pamenepo chinakomera atumwi ndi akulu ndi Mpingo wonse kusankha anthu a m'gulu lao, ndi kuwatumiza ku Antiokeya ndi Paulo ndi Barnabasi; ndiwo Yudasi wotchedwa Barsabasi, ndi Silasi, akulu a mwa abale; ndipo analembera mau natumiza ndi iwo: Atumwi ndi abale akulu kwa abale a mwa amitundu a m'Antiokeya, ndi Siriya, ndi Silisiya, tikulankhulani: Popeza tamva kuti ena amene anatuluka mwa ife anakuvutani ndi mau, nasocheretsa mitima yanu; amenewo sitinawalamulira; chinatikomera ndi mtima umodzi, tisankhe anthu, ndi kuwatumiza kwa inu pamodzi ndi okondedwa anthu Barnabasi ndi Paulo, anthu amene anapereka moyo wao chifukwa cha dzina la Yesu Khristu Ambuye wathu. Tatumiza tsono Yudasi ndi Silasi, omwenso adzakuuzani ndi mau zinthu zomwezo. Pakuti chinakomera Mzimu Woyera ndi ife, kuti tisasenzetse inu chothodwetsa chachikulu china choposa izi zoyenerazi; kuti musale nsembe za mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama; ngati mudzisungitsa pa zimenezi, kudzakhala bwino kwa inu. Tsalani bwino. Tsono pamene iwo anamuka anatsikira ku Antiokeya; ndipo anasonkhanitsa khamu, napereka kalatayo. Pamene anawerenga, anakondwera chifukwa cha chisangalatso chake. Ndipo Yudasi ndi Silasi, okhala eni okha aneneri, anasangalatsa abale ndi mau ambiri, nawalimbikitsa. Pamene anakhala nthawi, abale analawirana nao ndi mtendere amuke kwa iwo amene anawatumiza. *** Koma Paulo ndi Barnabasi anakhalabe m'Antiokeya, nalinkuphunzitsa, ndi kulalikira mau a Ambuye pamodzi ndi ena ambiri. Patapita masiku, Paulo anati kwa Barnabasi, Tibwerenso, tizonde abale m'midzi yonse m'mene tinalalikiramo mau a Ambuye, tione mkhalidwe wao. Ndipo Barnabasi anafuna kumtenga Yohane uja, wotchedwa Marko Koma sikunamkomera Paulo kumtenga iye amene anawasiya nabwerera pa Pamfiliya paja osamuka nao kuntchito. Ndipo panali kupsetsana mtima, kotero kuti analekana wina ndi mnzake; ndipo Barnabasi anatenga Marko, nalowa m'ngalawa, nanka ku Kipro. Koma Paulo anasankha Silasi, namuka, woikizidwa ndi abale ku chisomo cha Ambuye. Ndipo iye anapita kupyola pa Siriya ndi Silisiya, nakhazikitsa Mipingo. Ndipo anafikanso ku Deribe ndi Listara; ndipo taonani, panali wophunzira wina pamenepo, dzina lake Timoteo, amake ndiye Myuda wokhulupirira; koma atate wake ndiye Mgriki. Ameneyo anamchitira umboni wabwino abale a ku Listara ndi Ikonio. Iyeyo Paulo anafuna kuti amuke naye, ndipo anamtenga, namdula, chifukwa cha Ayuda amene anakhala m'maikomo; pakuti onse anadziwa kuti atate wake anali Mgriki. Pamene anapita kupyola pamidzi, anapereka kwa iwo malamulo awasunge, amene analamulira atumwi ndi akulu a pa Yerusalemu. Kotero Mipingoyo inalimbikitsidwa m'chikhulupiriro, nachuluka m'chiwerengo chao tsiku ndi tsiku. Ndipo anapita pa dziko la Frijiya ndi Galatiya, atawaletsa Mzimu Woyera kuti asalalikire mau m'Asiya; pamene anafika kundunji kwa Misiya, anayesa kunka ku Bitiniya; ndipo Mzimu wa Yesu sanawaloleza; ndipo pamene anapita pambali pa Misiya, anatsikira ku Troasi. Ndipo masomphenya anaonekera kwa Paulo usiku: Panali munthu wa ku Masedoniya alinkuimirira, namdandaulira kuti, Muolokere ku Masedoniya kuno, mudzatithangate ife. Pamene anaona masomphenyawo, pomwepo tinayesa kutulukira kunka ku Masedoniya, poganizira kuti Mulungu anaitanira ife kulalikira Uthenga Wabwino kwa iwo. Chotero tinachokera ku Troasi m'ngalawa, m'mene tinalunjikitsa ku Samotrase, ndipo m'mawa mwake ku Neapoli; pochokera kumeneko tinafika ku Filipi, mudzi wa ku Masedoniya, waukulu wa m'dzikomo, wa milaga ya Roma; ndipo tidagona momwemo masiku ena. Tsiku la Sabata tinatuluka kumudzi kunka kumbali ya mtsinje, kumene tinaganizira kuti amapempherako; ndipo tinakhala pansi ndi kulankhula ndi akazi amene adasonkhana. Ndipo anatimva mkazi wina dzina lake Lidia, wakugulitsa chibakuwa, wa kumudzi wa Tiatira, amene anapembedza Mulungu; mtima wake Ambuye anatsegula; kuti amvere zimene anazinena Paulo. Pamene anabatizidwa iye ndi a pabanja pake anatidandaulira ife, kuti, Ngati mwandiyesera ine wokhulupirika kwa Ambuye, mulowe m'nyumba yanga, mugone m'menemo. Ndipo anatiumiriza ife. Ndipo panali, pamene tinali kunka kukapemphera, anakomana ndi ife mdzakazi wina amene anali ndi mzimu wambwebwe, amene anapindulira ambuye ake zambiri pakubwebweta pake. Ameneyo anatsata Paulo ndi ife, nafuula, kuti, Anthu awa ndi akapolo a Mulungu wa Kumwambamwamba, amene akulalikirani inu njira ya chipulumutso. Ndipo anachita chotero masiku ambiri. Koma Paulo anavutika mtima ndithu, nacheuka, nati kwa mzimuwo, Ndikulamulira iwe m'dzina la Yesu Khristu, tuluka mwa iye. Ndipo unatuluka nthawi yomweyo. Koma pamene ambuye ake anaona kuti kulingalira kwa kupindula kwao kwatha, anagwira Paulo ndi Silasi, nawakokera kunka nao kubwalo kwa akulu, ndipo pamene adanka nao kwa oweruza, anati, Anthu awa avuta kwambiri mudzi wathu, ndiwo Ayuda, ndipo alalikira miyambo imene siiloleka ife kuilandira, kapena kuichita, ndife Aroma. Ndipo linagumukira iwo khamulo; ndipo oweruza anawang'ambira malaya ao; nalamulira kuti awakwapule. Pamene anawaonetsa mikwingwirima yambiri, anawaika m'ndende, nauza mdindo kuti awasunge bwino. Pakumva iye kulamulira kotero anawaika m'chipinda cha m'kati, namangitsa mapazi ao m'zigologolo. Koma ngati pakati pa usiku, Paulo ndi Silasi analinkupemphera, naimbira Mulungu nyimbo, ndipo a m'ndendemo analinkuwamva; ndipo mwadzidzidzi panali chivomezi chachikulu, chotero kuti maziko a ndende anagwedezeka: pomwepo pamakomo ponse panatseguka; ndi maunyolo a onse anamasuka. Pamene anautsidwa kutulo mdindoyo, anaona kuti pa makomo a ndende panatseguka, ndipo anasolola lupanga lake, nati adziphe yekha, poyesa kuti am'ndende adathawa. Koma Paulo anafuula ndi mau akulu, nati, Usadzipweteka wekha; tonse tili muno. Ndipo mdindo anaitanitsa nyali, natumphira m'kati, alinkunthunthumira ndi mantha, nagwa pamaso pa Paulo ndi Silasi, nawatulutsira iwo kunja, nati, Ambuye, ndichitenji kuti ndipulumuke? Ndipo iwo anati, Ukhulupirire Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka, iwe ndi apabanja ako. Ndipo anamuuza iye mau a Ambuye, pamodzi ndi onse a pabanja pake. Ndipo anawatenga ora lomwelo la usiku, natsuka mikwingwirima yao; nabatizidwa pomwepo, iye ndi a pabanja pake. Ndipo anakwera nao kunka kunyumba kwake, nawakhazikira chakudya, nasangalala kwambiri, pamodzi ndi a pabanja pake, atakhulupirira Mulungu. Kutacha, oweruza anatumiza akapitao, kuti, Mukamasule anthu aja. Ndipo mdindo anafotokozera mauwo kwa Paulo, nati, Oweruza atumiza mau kunena kuti mumuke; tsopanotu tulukani, mukani mumtendere. Koma Paulo anati kwa iwo, Adatikwapula ife pamaso pa anthu, osamva mlandu wathu, ife amene tili Aroma, natiika m'ndende; ndipo tsopano kodi afuna kutitulutsira ife m'tseri? Iai, ndithu; koma adze okha atitulutse. Ndipo akapitao anafotokozera mauwo kwa oweruza; ndipo iwowo anaopa, pakumva kuti anali Aroma. Ndipo anadza nawapembedza; ndipo pamene anawatulutsa, anawapempha kuti achoke pamudzi. Ndipo anatuluka m'ndendemo, nalowa m'nyumba ya Lidia: ndipo pamene anaona abale, anawasangalatsa, namuka. Pamene anapitirira pa Amfipoli, ndi Apoloniya, anafika ku Tesalonika, kumene kunali sunagoge wa Ayuda. Ndipo Paulo, monga amachita, analowa kwa iwo; ndipo masabata atatu ananena ndi iwo za m'malembo, natanthauzira, natsimikiza, kuti kunayenera Khristu kumva zowawa, ndi kuuka kwa akufa; ndiponso kuti Yesu yemweyo, amene ndikulalikirani inu, ndiye Khristu. Ndipo ena a iwo anakopedwa, nadziphatika kwa Paulo ndi Silasi; ndi Agriki akupembedza aunyinji ndithu, ndi akazi akulu osati owerengeka. Koma Ayuda anadukidwa mtima, natenga anthu ena oipa achabe a pabwalo, nasonkhanitsa khamu la anthu, nachititsa phokoso m'mudzi; ndipo anagumukira kunyumba ya Yasoni, nafuna kuwatulutsira kwa anthu. Pamene sanawapeza anakokera Yasoni ndi abale ena pamaso pa akulu a mudzi, nafuula kuti, Omwe aja asanduliza dziko lokhalamo anthu, afika kunonso; amene Yasoni walandira; ndipo onsewo achita zokana malamulo a Kaisara; nanena kuti pali mfumu ina, Yesu. Ndipo anavuta anthu, ndi akulu a mudzi, pamene anamva zimenezi. Ndipo pamene analandira chikole kwa Yasoni ndi enawo, anawamasula. Pomwepo abale anatumiza Paulo ndi Silasi usiku kunka ku Berea; pamene iwo anafika komweko analowa m'sunagoge wa Ayuda. Amenewa anali mfulu koposa a m'Tesalonika, popeza analandira mau ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m'malembo masiku onse, ngati zinthu zinali zotero. Ndipo ambiri a iwo anakhulupirira; ndi akazi a Chigriki omveka, ndi amuna, osati owerengeka. Koma pamene Ayuda a ku Tesalonika anazindikira kuti mau a Mulungu analalikidwa ndi Paulo ku Bereanso, anadza komwekonso, nautsa, navuta makamu. Pomwepo abale anatulutsa Paulo amuke kufikira kunyanja; koma Silasi ndi Timoteo anakhalabe komweko. Koma iwo amene anaperekeza Paulo anadza naye kufikira ku Atene; ndipo polandira iwo lamulo la kwa Silasi ndi Timoteo kuti afulumire kudza kwa iye ndi changu chonse, anachoka. Pamene Paulo analandira iwo pa Atene, anavutidwa mtima pamene anaona mudzi wonse wadzala ndi mafano. Chotero tsono anatsutsana ndi Ayuda ndi akupembedza m'sunagoge, ndi m'bwalo la malonda masiku onse ndi iwo amene anakomana nao. Ndipo akukonda nzeru ena a Epikurea ndi a Stoiki anatengana naye. Ena anati, Ichi chiyani afuna kunena wobwetuka uyu? Ndipo ena, Anga wolalikira ziwanda zachilendo, chifukwa analalikira Yesu ndi kuuka kwa akufa. Ndipo anamgwira, nanka naye ku Areopagi, nati, Kodi tingathe kudziwa chiphunzitso ichi chatsopano uchinena iwe? Pakuti ufika nazo kumakutu athu zachilendo: tifuna tsono kudziwa, izi zitani? (Koma Aatene onse ndi alendo akukhalamo anakhalitsa nthawi zao, osachita kanthu kena koma kunena kapena kumva cha tsopano.) Ndipo anaimirira Paulo pakati pa Areopagi nati, Amuna inu a Atene, m'zinthu zonse ndiona kuti muli akupembedzetsa. Pakuti popita, ndi kuona zinthu zimene muzipembedza, ndipezanso guwa la nsembe lolembedwa potere, KWA MULUNGU WOSADZIWIKA. Chimene muchipembedza osachidziwa, chimenecho ndichilalikira kwa inu. Mulungu amene analenga dziko lapansi ndi zonse zili momwemo, Iyeyo, ndiye mwini kumwamba ndi dziko lapansi, sakhala m'nyumba za kachisi zomangidwa ndi manja; satumikiridwa ndi manja a anthu, monga wosowa kanthu, popeza Iye mwini apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse; ndipo ndi mmodzi analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi, atapangiratu nyengo zao, ndi malekezero a pokhala pao; kuti afunefune Mulungu, kapena akamfufuze ndi kumpeza, ngakhale sakhala patali ndi yense wa ife; pakuti mwa Iye tikhala ndi moyo ndi kuyendayenda, ndi kupeza mkhalidwe wathu; monga enanso a akuimba anu ati, Pakuti ifenso tili mbadwa zake. Popeza tsono tili mbadwa za Mulungu, sitiyenera kulingalira kuti umulungu uli wofanafana ndi golide, kapena siliva, kapena mwala, wolocha ndi luso ndi zolingalira za anthu. Nthawi za kusadziwako tsono Mulungu analekerera; koma tsopanotu alinkulamulira anthu onse ponseponse atembenuke mtima; chifukwa anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m'chilungamo, ndi munthu amene anamuikiratu; napatsa anthu onse chitsimikizo, pamene anamuukitsa Iye kwa akufa. Ndipo pamene anamva za kuuka kwa akufa ena anaseka pwepwete; koma ena anati, Tidzakumvanso za chimenechi. Choncho Paulo anatuluka pakati pao. Koma ena anadziphatika kwa iye, nakhulupirira; mwa iwonso munali Dionizio Mwareopagi, ndi mkazi dzina lake Damarisi, ndi ena pamodzi nao. Zitapita izi anachoka ku Atene, nadza ku Korinto. Ndipo anapeza Myuda wina dzina lake Akwila, fuko lake la ku Ponto, atachoka chatsopano ku Italiya, pamodzi ndi mkazi wake Prisila, chifukwa Klaudio analamulira Ayuda onse achoke m'Roma; ndipo Paulo anadza kwa iwo: ndipo popeza anali wa ntchito imodzimodzi, anakhala nao, ndipo iwowa anagwira ntchito; pakuti ntchito yao inali yakusoka mahema. Ndipo anafotokozera m'sunagoge masabata onse, nakopa Ayuda ndi Agriki. Koma pamene Silasi ndi Timoteo anadza potsika ku Masedoniya, Paulo anapsinjidwa ndi mau, nachitira umboni kwa Ayuda kuti Yesu ndiye Khristu. Koma pamene iwo, anamkana, nachita mwano, anakutumula malaya ake, nati kwa iwo, Mwazi wanu ukhale pa mitu yanu; ine ndilibe kanthu; kuyambira tsopano ndinka kwa amitundu. Ndipo anachoka kumeneko, nalowa m'nyumba ya munthu, dzina lake Tito Yusto, amene anapembedza Mulungu, nyumba yake inayandikizana ndi sunagoge. Ndipo Krispo, mkulu wa sunagoge, anakhulupirira Ambuye, ndi apabanja ake onse; ndipo Akorinto ambiri anamva, nakhulupirira, nabatizidwa. Ndipo Ambuye anati kwa Paulo usiku m'masomphenya, Usaope, koma nena, usakhale chete; chifukwa Ine ndili pamodzi ndi iwe, ndipo palibe munthu adzautsana ndi iwe kuti akuipse; chifukwa ndili nao anthu ambiri m'mudzi muno. Ndipo anakhala komwe chaka chimodzi kudza miyezi isanu ndi umodzi; naphunzitsa mau a Mulungu mwa iwo. Tsono pamene Galio anali chiwanga cha Akaya, Ayuda ndi mtima umodzi anamuukira Paulo, nanka naye kumpando wachiweruziro, kuti, Uyu akopa anthu apembedze Mulungu pokana chilamulo. Koma pamene Paulo anati atsegule pakamwa pake, Galio anati kwa Ayuda, Ukadakhala mlandu wa chosalungama, kapena dumbo loipa, Ayuda inu, mwenzi nditakumverani inu; koma akakhala mafunso a mau ndi maina ndi chilamulo chanu; muyang'ane inu nokha; sindifuna kuweruza zimenezi. Ndipo anawapirikitsa pa mpando wachiweruziro. Ndipo anamgwira Sostene, mkulu wa sunagoge, nampanda kumpando wachiweruziro. Ndipo Galio sanasamalira zimenezi. Paulo atakhala chikhalire masiku ambiri, anatsazika abale, nachoka pamenepo, napita m'ngalawa ku Siriya, pamodzi naye Prisila ndi Akwila; popeza anameta mutu wake m'Kenkrea; pakuti adawinda. Ndipo iwo anafika ku Efeso, ndipo iye analekana nao pamenepo: koma iye yekha analowa m'sunagoge, natsutsana ndi Ayuda. Pamene iwo anamfunsa iye kuti akhale nthawi ina yoenjezerapo, sanavomereza; koma anawatsanzika, nati, Akafuna Mulungu, ndidzabwera kwa inu; ndipo anachoka ku Efeso m'ngalawa. Ndipo pamene anakocheza pa Kesareya, anakwera naulonjera Mpingo, natsikira ku Antiokeya. Atakhala kumeneko nthawi, anachoka, napita ku madera osiyanasiyana a dziko la Galatiya ndi la Frijiya, nakhazikitsa ophunzira onse. Ndipo anafika ku Efeso Myuda wina dzina lake Apolo, fuko lake la ku Aleksandriya, munthu wolankhula mwanzeru; ndipo anali wamphamvu m'malembo. Iyeyo anaphunzitsidwa m'njira ya Ambuye; pokhala nao mzimu wachangu, ananena ndi kuphunzitsa mosamalira zinthu za Yesu, ndiye wodziwa ubatizo wa Yohane wokha; ndipo iye anayamba kulankhula molimba mtima m'sunagoge, koma pamene anamumva iye Prisila ndi Akwila, anamtenga, namfotokozera njira ya Mulungu mosamalitsa. Ndipo pamene iye anafuna kuoloka kunka ku Akaya, abale anamfulumiza, ndi kulembera akalata kwa ophunzira kuti amlandire: ndipo pamene anafika, iye anathangata ndithu iwo akukhulupirira mwa chisomo; pakuti ndi mphamvu anatsutsa Ayuda, pamaso pa anthu, nasonyeza mwa malembo kuti Yesu ndiye Khristu. Ndipo panali, pamene Apolo anali ku Korinto, Paulo anapita pa maiko a pamtunda, nafika ku Efeso, napeza ophunzira ena; ndipo anati kwa iwo, Kodi munalandira Mzimu Woyera pamene munakhulupirira? Ndipo anati, Iai, sitinamva konse kuti Mzimu Woyera waperekedwa. Ndipo anati, Nanga mwabatizidwa m'chiyani? Ndipo anati, Mu ubatizo wa Yohane. Ndipo anati Paulo, Yohane anabatiza ndi ubatizo wa kutembenuka mtima, nati kwa anthu, kuti amkhulupirire Iye amene adzadza pambuyo pake, ndiye Yesu. Pamene anamva ichi, anabatizidwa m'dzina la Ambuye Yesu. Ndipo pamene Paulo anaika manja ake pa iwo, Mzimu Woyera anadza pa iwo; ndipo analankhula ndi malilime, nanenera. Onsewo anali ngati amuna khumi ndi awiri. Ndipo iye analowa m'sunagoge, nanena molimba mtima, miyezi itatu, natsutsana ndi kukopa kunena za Ufumu wa Mulungu. Koma pamene ena anaumitsa mtima ndi kusamvera, nanenera zoipa Njirayo pamaso pa anthu, anawachokera, napatutsa ophunzira, nafotokozera masiku onse m'sukulu ya Tirano. Ndipo anachita chomwecho zaka ziwiri; kotero kuti onse akukhala m'Asiya anamva mau a Ambuye, Ayuda ndi Agriki. Ndipo Mulungu anachita zamphamvu za pa zokha ndi manja a Paulo; kotero kuti anamuka nazo kwa odwala nsalu zopukutira ndi za pantchito, zochokera pathupi pake, ndipo nthenda zinawachokera, ndi ziwanda zinatuluka. Koma Ayuda enanso oyendayenda, otulutsa ziwanda, anadziyesa kutchula pa iwo amene anali ndi ziwanda dzina la Ambuye Yesu, kuti, Ndikulumbirirani pa Yesu amene amlalika Paulo. Ndipo panali ana amuna asanu ndi awiri a Skeva, Myuda, mkulu wa ansembe amene anachita ichi. Ndipo unayankha mzimu woipa, nuti kwa iwo, Yesu ndimzindikira, ndi Paulo ndimdziwa, koma inu ndinu ayani? Ndipo munthu, mwa iye amene munali mzimu woipa, anawalumphira nawaposa, nawalaka onse awiriwo, kotero kuti anathawa m'nyumba amaliseche ndi olasidwa. Zimenezo zidamveka kwa onse, Ayuda ndi Agriki, amene anakhala ku Efeso; ndipo mantha anagwera onsewo, ndipo dzina la Ambuye Yesu linakuzika. Ndipo ambiri a iwo akukhulupirirawo anadza, navomereza, nafotokoza machitidwe ao. Ndipo ambiri a iwo akuchita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku ao, nawatentha pamaso pa onse; ndipo anawerenga mtengo wake, napeza ndalama zasiliva zikwi makumi asanu. Chotero mau a Ambuye anachuluka mwamphamvu nalakika. Ndipo zitatha izi, Paulo anatsimikiza mu mzimu wake, atapita pa Masedoniya ndi Akaya, kunka ku Yerusalemu, kuti, Nditamuka komweko ndiyenera kuonanso ku Roma. Pamene anatuma ku Masedoniya awiri a iwo anamtumikira, Timoteo ndi Erasto, iye mwini anakhalabe nthawi m'Asiya. Nthawi yomweyo kunali phokoso lambiri kunena za Njirayo. Pakuti munthu wina dzina lake Demetrio wosula siliva, amene anapanga tiakachisi tasiliva, ta Aritemi, anaonetsera amisiri phindu lambiri; amenewo iye anawasonkhanitsa pamodzi ndi amisiri a ntchito yomweyo, nati, Amuna inu, mudziwa kuti ndi malonda awa ife tipeza chuma chathu. Ndipo muona ndi kumva, kuti si pa Efeso pokha, koma monga pa Asiya ponse, Paulo uyu akopa ndi kutembenutsa anthu ambiri, ndi kuti, Si milungu iyi imene ipangidwa ndi manja: ndipo tiopa ife kuti ntchito yathuyi idzayamba kunyonyosoka; komanso kuti Kachisi wa mulungu wamkazi Aritemi adzayamba kuyesedwa wachabe; ndiponso kuti iye adzayamba kutsitsidwa ku ukulu wake, iye amene a m'Asiya onse, ndi onse a m'dziko lokhalamo anthu, ampembedza. Ndipo pamene anamva, anadzala ndi mkwiyo, nafuula, nati, Wamkulu ndi Aritemi wa ku Efeso. Ndipo m'mudzi monse munachita piringupiringu, nathamangira onse pamodzi ku bwalo losewera, atagwira Gayo ndi Aristariko, anthu a ku Masedoniya, alendo anzake a Paulo. Ndipo pamene Paulo anafuna kulowa kwa anthu, ophunzira ake sanamloleza. Ndipo akulu ena a Asiyanso, popeza anali abwenzi ake, anatumiza mau kwa iye, nampempha asadziponye kubwalo lakusewera. Ndipo ena anafuula kanthu kena, ena kanthu kena; pakuti msonkhanowo unasokonezeka; ndipo unyinji sunadziwa chifukwa chake cha kusonkhana. Ndipo anatulutsa Aleksandro m'khamumo, kumtulutsa iye Ayuda. Ndipo Alesandro anatambasula dzanja, nafuna kudzikanira kwa anthu adasonkhanawo. Koma pozindikira kuti ali Myuda, kunali mau amodzi a kwa onse akufuula monga maora awiri, Wamkulu ndi Aritemi wa Aefeso. Ndipo pamene mlembi adatontholetsa khamulo, anati, Amuna a Efeso inu, munthuyu ndani wosadziwa kuti mudzi wa Aefeso ndiwo wosungira Kachisi wa Aritemi wamkulu, ndi fano lidachokera kwa Zeusi? Popeza tsono izi sizikanika, muyenera inu kukhala chete, ndi kusachita kanthu kaliuma. Pakuti mwatenga anthu awa, osakhala olanda za m'Kachisi, kapena ochitira mulungu wathu mwano. Ngati tsono Demetrio ndi amisiri okhala naye, ali ndi mlandu ndi munthu, mabwalo a milandu alipo, ndi ziwanga zilipo; anenezane. Koma ngati mufuna kanthu ka zinthu zina, kadzakonzeka m'msonkhano wolamulidwa. Pakutinso palipo potiopsa kuti adzatineneza za chipolowe chalero; popeza palibe chifukwa cha kufotokozera za chipiringu chimene. Ndipo pamene ananena izi, anamasula msonkhano. Ndipo litaleka phokoso, Paulo anaitana ophunzirawo, ndipo m'mene anawachenjeza, analawirana nao, natuluka kunka ku Masedoniya. Ndipo m'mene atapitapita m'mbali zijazo, nawachenjeza, anadza ku Grisi. Ndipo m'mene adakhalako miyezi itatu, ndipo atampangira chiwembu Ayuda, poti iye apite ndi ngalawa ku Siriya, anatsimikiza mtima abwerere popyola Masedoniya. Ndipo anamperekeza kufikira ku Asiya Sopatere mwana wa Piro, wa ku Berea; ndipo a Atesalonika, Aristariko ndi Sekundo; ndi Gayo wa ku Deribe, ndi Timoteo; ndi a ku Asiya, Tikiko ndi Trofimo. Koma iwowa adatitsogolera, natilinda ku Troasi. Ndipo tinapita m'ngalawa kuchokera ku Filipi, atapita masiku a mkate wopanda chotupitsa, ndipo popita masiku asanu tinawapeza ku Troasi; pamenepo tinatsotsa masiku asanu ndi awiri. Ndipo tsiku loyamba la sabata, posonkhana ife kunyema mkate, Paulo anawafotokozera mau, popeza anati achoke m'mawa mwake; ndipo ananena chinenere kufikira pakati pa usiku. Ndipo munali nyali zambiri m'chipinda chapamwamba m'mene tinasonkhanamo. Ndipo mnyamata dzina lake Yutiko anakhala pazenera, wogwidwa nato tulo tatikulu; ndipo pakukhala chifotokozere Paulo, ndipo pogwidwa nato tulo, anagwa posanja pachiwiri, ndipo anamtola wakufa. Ndipo potsikirako Paulo, anamgwera namfungatira, nati, Musachite phokoso, pakuti moyo wake ulipo. Ndipo m'mene adakwera, nanyema mkate, nadya, nakamba nao nthawi, kufikira kucha, anachokapo. Ndipo anadza naye mnyamata ali wamoyo, natonthozedwa kwakukulu. Koma ife tinatsogolera kunka kungalawa, ndipo tinapita ku Aso, pamenepo tinati timlandire Paulo; pakuti anatipangira chomwecho, koma anati ayenda pamtunda yekha. Ndipo pamene anakomana ndi ife ku Aso, tinamlandira, ndipo tinafika ku Mitilene. Ndipo m'mene tidachokerapo, m'mawa mwake tinafika pandunji pa Kiyo; ndi m'mawa mwake tinangokocheza ku Samo, ndi m'mawa mwake tinafika ku Mileto. Pakuti Paulo adatsimikiza mtima apitirire pa Efeso, angataye nthawi m'Asiya; pakuti anafulumira, ngati kutheka, akhale ku Yerusalemu tsiku la Pentekoste. Ndipo pokhala ku Mileto anatuma ku Efeso, naitana akulu a Mpingo. Ndipo pamene anafika kuli iye, anati kwa iwo, Mudziwa inu kuyambira tsiku loyamba ndinafika ku Asiya, makhalidwe anga pamodzi ndi inu nthawi yonse, wotumikira Ambuye ndi kudzichepetsa konse ndi misozi, ndi mayesero anandigwera ndi ziwembu za Ayuda; kuti sindinakubisirani zinthu zopindulira, osazilalikira kwa inu, ndi kukuphunzitsani inu pabwalo ndi m'nyumba zanu, ndi kuchitira umboni Ayuda ndi Agriki wa kutembenuka mtima kulinga kwa Mulungu, ndi chikhulupiriro cholinga kwa Ambuye wathu Yesu Khristu. Ndipo, taonani, ndipita ku Yerusalemu womangidwa mumzimu, wosadziwa zimene zidzandigwera ine kumeneko; koma kuti Mzimu Woyera andichitira umboni m'midzi yonse, ndi kunena kuti nsinga ndi zisautso zindilindira. Komatu sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kuchitira umboni Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu. Ndipo tsopano, taonani, ndidziwa ine kuti inu nonse amene ndinapitapita mwa inu kulalikira ufumuwo, simudzaonanso nkhope yanga. Chifukwa chake ndikuchitirani umboni lero lomwe, kuti ndilibe kanthu ndi mwazi wa anthu onse. Pakuti sindinakubisirani pakukulalikirani uphungu wonse wa Mulungu. Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang'anira, kuti muwete Mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa Iye yekha. Ndidziwa ine kuti, nditachoka ine, adzalowa mimbulu yosautsa, yosalekerera gululo; ndipo mwa inu nokha adzauka anthu, olankhula zokhotakhota, kupatutsa ophunzira awatsate. Chifukwa chake dikirani, nimukumbukire kuti zaka zitatu sindinaleka usiku ndi usana kuchenjeza yense wa inu ndi misozi. Ndipo tsopano ndikuikizani kwa Mulungu, ndi kwa mau a chisomo chake, chimene chili ndi mphamvu yakumangirira ndi kupatsa inu cholowa mwa onse oyeretsedwa. Sindinasirira siliva, kapena golide, kapena chovala cha munthu aliyense. Mudziwa inu nokha kuti manja anga awa anatumikira zosowa zanga, ndi za iwo akukhala ndi ine. M'zinthu zonse ndinakupatsani chitsanzo, chakuti pogwiritsa ntchito, kotero muyenera kuthandiza ofooka ndi kukumbuka mau a Ambuye Yesu, kuti anati yekha, Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira. Ndipo m'mene ananena izi, anagwada pansi, napemphera ndi iwo onse. Ndipo onsewa analira kwambiri, namkupatira Paulo pakhosi pake, nampsompsona, nalira makamaka chifukwa cha mau adanenawa, kuti sadzaonanso nkhope yake. Ndipo anamperekeza iye kungalawa. Ndipo kunali, titalekana nao ndi kukankha ngalawa, tinadza molunjika ku Kosi, ndi m'mawa mwake ku Rode, ndipo pochokerapo ku Patara; ndipo m'mene tinapeza ngalawa yakuoloka kunka ku Fenisiya, tinalowamo, ndi kupita nayo. Ndipo pamene tinafika popenyana ndi Kipro, tinachisiya kulamanzere, nkupita ku Siriya; ndipo tinakocheza ku Tiro; pakuti pamenepo ngalawa inafuna kutula akatundu ake. Ndipo m'mene tinapeza ophunzira, tinakhalako masiku asanu ndi awiri; ndipo iwowa ananena ndi Paulo mwa Mzimu, kuti asakwere ku Yerusalemu. Ndipo kunali pamene tidatsiriza masikuwa, tidachoka ndi kunka ulendo wathu; ndipo iwo onse, akazi ndi ana, anatiperekeza kufikira kutuluka m'mudzi; ndipo pogwadira pa mchenga wa kunyanja, tinapemphera, ndi kulawirana; ndipo tinalowa m'ngalawa, koma iwo anabwera kwao. Ndipo ife titatsiriza ulendo wathu wochokera ku Tiro, tinafika ku Ptolemaisi; ndipo m'mene tidalonjera abale, tinakhala nao tsiku limodzi. Ndipo m'mawa mwake tinachoka, ndipo tinafika ku Kesareya, ndipo m'mene tinalowa m'nyumba ya Filipo mlaliki, mmodzi wa asanu ndi awiri aja, tinakhala naye. Ndipo munthuyu anali nao ana akazi anai, anamwali, amene ananenera. Ndipo pokhalapo masiku ambiri, anatsika ku Yudeya mneneri, dzina lake Agabu. Ndipo anadza kwa ife natenga lamba la Paulo, nadzimanga yekha manja ndi mapazi, nati, Atero Mzimu Woyera, Munthu mwini lamba ili, adzammanga kotero Ayuda a m'Yerusalemu, nadzampereka m'manja a amitundu. Koma pamene tinamva izi tinamdandaulira ife ndi iwo a komweko, asakwere iye kunka ku Yerusalemu. Pamenepo Paulo anayankha, Muchitanji, polira ndi kundiswera mtima? Pakuti ndakonzeka ine si kumangidwa kokha, komatunso kufera ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu. Ndipo pokana iye kukopeka, tinaleka, ndi kuti, Kufuna kwa Ambuye kuchitidwe. Ndipo atapita masiku awa tinakonza akatundu athu, ntikwera ku Yerusalemu. Ndipo anamuka nafenso ena a ophunzira a ku Kesareya, natenganso wina Mnasoni wa ku Kipro, wophunzira wakale, amene adzatichereza. Ndipo pofika ife ku Yerusalemu, abale anatilandira mokondwera. Ndipo m'mawa mwake Paulo analowa nafe kwa Yakobo; ndi akulu onse anali pomwepo. Ndipo atawalonjera iwo, anawafotokozera chimodzichimodzi zimene Mulungu anachita kwa amitundu mwa utumiki wake. Ndipo pamene anazimva, analemekeza Mulungu; nati kwa iye, Uona, mbale, kuti ambirimbiri mwa Ayuda akhulupirira; ndipo ali nacho changu onsewa, cha pa chilamulo; ndipo anamva za iwe, kuti uphunzitsa Ayuda onse a kwa amitundu apatukane naye Mose, ndi kuti asadule ana ao, kapena asayende monga mwa miyambo. Nchiyani tsono? Adzamva ndithu kuti wafika. Chifukwa chake uchite ichi tikuuza iwe; tili nao amuna anai amene anawinda; amenewa uwatenge nudziyeretse nao pamodzi, nuwalipirire, kuti amete mutu; ndipo adzadziwa onse kuti zomveka za iwe nzachabe, koma kuti iwe wekhanso uyenda molunjika, nusunga chilamulo. Koma kunena za amitundu adakhulupirirawo, tinalembera ndi kulamulira kuti asale zoperekedwa kwa mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama. Pamenepo Paulo anatenga anthuwo, ndipo m'mawa mwake m'mene anadziyeretsa nao pamodzi, analowa m'Kachisi, nauza chimalizidwe cha masiku a kuyeretsa, kufikira adawaperekera iwo onse mtulo. Ndipo pamene masiku asanu ndi awiri anati amalizidwe, Ayuda a ku Asiya pomuona iye m'Kachisi, anautsa khamu lonse la anthu, namgwira, nafuula, Amuna a Israele, tithandizeni; ameneyu ndi munthu uja anaphunzitsa onse ponsepo ponenera anthu, ndi chilamulo, ndi malo ano; ndiponso anatenga Agriki nalowa nao m'Kachisi, nadetsa malo ano oyera. Pakuti adaona Trofimo wa ku Efeso kale pamodzi ndi iye mumzinda; ameneyo anayesa kuti Paulo anamtenga nalowa naye ku Kachisi. Ndipo mudzi wonse unasokonezeka, ndipo anthu anathamangira pamodzi; nagwira Paulo namkoka kumtulutsa m'Kachisi; ndipo pomwepo pamakomo panatsekedwa. Ndipo m'mene anafuna kumupha iye, wina anamuuza kapitao wamkulu wa gululo kuti m'Yerusalemu monse muli piringupiringu. Ndipo posachedwa iye anatenga asilikali ndi akenturiyo, nathamanga, nawatsikira; ndipo iwowa, pakuona kapitao wamkulu ndi asilikali, analeka kumpanda Paulo. Pamenepo poyandikira kapitao wamkulu anamgwira iye, nalamulira ammange ndi maunyolo awiri; ndipo anafunsira, ndiye yani, ndipo anachita chiyani? Koma wina anafuula kena, wina kena, m'khamumo; ndipo m'mene sanathe kudziwa zoona chifukwa cha phokosolo analamulira amuke naye kulinga. Ndipo pamene anafika pamakwerero, kudatero kuti anamsenza asilikali chifukwa cha kulimbalimba kwa khamulo; pakuti unyinji wa anthu unatsata, nufuula, Mchotse iye. Ndipo poti alowe naye m'linga, Paulo ananena kwa kapitao wamkulu, Mundilole ndikuuzeni kanthu? Ndipo anati, Kodi udziwa Chigriki? Si ndiwe Mwejipito uja kodi, unachita mipanduko kale lija, ndi kutsogolera ambanda aja zikwi zinai kuchipululu? Koma Paulo anati, Ine ndine munthu Myuda, wa ku Tariso wa m'Silisiya, mfulu ya mudzi womveka; ndipo ndikupemphani mundilole ndilankhule ndi anthu. Ndipo m'mene adamlola, Paulo anaimirira pamakwerero, natambalitsira anthu dzanja; ndipo pokhala chete onse, analankhula nao m'chinenedwe cha Chihebri, nanena: Amuna, abale, ndi atate, mverani chodzikanira changa tsopano, cha kwa inu. Ndipo pakumva kuti analankhula nao m'chinenedwe cha Chihebri, anaposa kukhala chete; ndipo anati: Ine ndine munthu Myuda, wobadwa m'Tariso wa Silisiya, koma ndaleredwa m'mzinda muno, pa mapazi a Gamaliele, wolangizidwa monga mwa chitsatidwe chenicheni cha chilamulo cha makolo athu, ndipo ndinali wachangu, cholinga kwa Mulungu, monga muli inu nonse lero; ndipo ndinalondalonda Njira iyi kufikira imfa, ndi kumanga ndi kupereka kundende amuna ndi akazi. Monganso mkulu wa ansembe andichitira umboni, ndi bwalo lonse la akulu; kwa iwo amenenso ndinalandira akalata kunka nao kwa abale, ndipo ndinapita ku Damasiko, kuti ndikatenge iwonso akukhala kumeneko kudza nao omangidwa ku Yerusalemu, kuti alangidwe. Ndipo kunali, pakupita ine ndi kuyandikira ku Damasiko, monga usana, mwadzidzidzi kunandiwalira pondizungulira ine kuunika kwakukulu kochokera kumwamba. Ndipo ndinagwa pansitu, ndipo ndinamva mau akunena nane, Saulo, Saulo, undilondalonderanji Ine? Ndipo ndinayankha, Ndinu yani Mbuye? Ndipo anati kwa ine, Ndine Yesu wa ku Nazarete, amene umlondalonda. Ndipo iwo akukhala nane anaonadi kuunika, koma sanamva mau akulankhula nane. Ndipo ndinati, Ndidzachita chiyani, Ambuye? Ndipo Ambuye anati kwa ine, Tauka, pita ku Damasiko; kumeneko adzakufotokozera zonse zoikika kwa iwe uzichite. Ndipo popeza sindinapenya, chifukwa cha ulemerero wa kuunikako, anandigwira dzanja iwo amene anali ndi ine, ndipo ndinafika ku Damasiko. Ndipo munthu dzina lake Ananiya, ndiye munthu wopembedza monga mwa chilamulo, amene amchitira umboni wabwino Ayuda onse akukhalako, anadza kwa ine, ndipo poimirirapo anati kwa ine, Saulo, mbale, penyanso. Ndipo ine, ora lomweli ndinampenya. Ndipo anati, Mulungu wa makolo athu anakusankhiratu udziwe chifuniro chake, nuone Wolungamayo, numve mau otuluka m'kamwa mwake. Ndipo udzamkhalira Iye mboni kwa anthu onse, za izo udaziona ndi kuzimva. Ndipo tsopano uchedweranji? Tauka, nubatizidwe ndi kusamba kuchotsa machimo ako, nuitane pa dzina lake. Ndipo kunali, nditabwera ku Yerusalemu ndinalikupemphera m'Kachisi, ndinachita ngati kukomoka, ndipo ndinamuona Iye, nanena nane, Fulumira, tuluka msanga m'Yerusalemu; popeza sadzalandira umboni wako wakunena za Ine. Ndipo ndinati ine, Ambuye, adziwa iwo okha kuti ndinali kuika m'ndende ndi kuwapanda m'masunagoge onse iwo akukhulupirira Inu; ndipo pamene anakhetsa mwazi wa Stefano mboni yanu, ine ndemwe ndinalikuimirirako, ndi kuvomerezana nao, ndi kusunga zovala za iwo amene anamupha iye. Ndipo anati kwa ine, Pita; chifukwa Ine ndidzakutuma iwe kunka kutali kwa amitundu. Ndipo adamumva kufikira mau awa; ndipo anakweza mau ao nanena, Achoke pa dziko lapansi munthu wotere; pakuti sayenera iye kukhala ndi moyo. Ndipo pakufuula iwo, ndi kutaya zovala zao, ndi kuwaza fumbi mumlengalenga, kapitao wamkulu analamulira kuti amtenge iye kulowa naye kulinga, nati amfunsefunse ndi kumkwapula, kuti adziwe chifukwa chake nchiyani kuti amfuulira chomwecho. Ndipo m'mene anammanga iye ndi nsingazo, Paulo anati kwa kenturiyo wakuimirirako, Kodi nkuloleka kwa inu kukwapula munthu Mroma, mlandu wake wosamveka? Ndipo pakumva ichi kenturiyoyo, ananka kwa kapitao wamkulu, namuuza, nanena, Nchiyani ichi uti uchite? Pakuti munthuyo ndiye Mroma. Ndipo kapitao wamkuluyo anadza, nati kwa iye, Ndiuze, iwe ndiwe Mroma kodi? Ndipo anati, Inde. Ndipo kapitao wamkulu anayankha, Ine ndalandira ufulu umene ndi kuperekapo mtengo wake waukulu. Ndipo Paulo anati, Koma ine ndabadwa Mroma. Pamenepo ndipo iwo amene anati amfunsefunse, anamsiya; ndipo kapitao wamkulunso anaopa, pozindikira kuti ndiye Mroma, ndiponso popeza adammanga iye. Koma m'mawa mwake pofuna kuzindikira chifukwa chake chenicheni chakuti anamnenera Ayuda, anammasula iye, nalamulira asonkhane ansembe aakulu, ndi bwalo lonse la akulu, ndipo anatsika naye Paulo, namuika pamaso pao. Ndipo Paulo, popenyetsetsa a m'bwalo la akulu anati, Amuna, abale, ndakhala ine pamaso pa Mulungu ndi chikumbu mtima chokoma chonse kufikira lero lomwe. Ndipo mkulu wa ansembe Ananiya analamulira akuimirirako ampande pakamwa pake. Pamenepo Paulo anati kwa iye, Mulungu adzakupanda iwe, khoma loyeretsedwa iwe; ndipo kodi ukhala iwe wakundiweruza mlandu monga mwa chilamulo, ndipo ulamulira andipande ine posanga chilamulo? Ndipo iwo akuimirirako anati, Ulalatira kodi mkulu wa ansembe wa Mulungu? Ndipo Paulo anati, Sindinadziwa, abale, kuti ndiye mkulu wa ansembe; pakuti kwalembedwa, Usamnenera choipa mkulu wa anthu ako. Koma pozindikira Paulo kuti ena ndi Asaduki, ndi ena Afarisi, anafuula m'bwalomo, Amuna, abale, ine ndine Mfarisi, mwana wa Afarisi: andinenera mlandu wa chiyembekezo ndi kuuka kwa akufa. Ndipo pamene adatero, kunakhala chilekano pakati pa Afarisi ndi Asaduki; ndipo osonkhanawo anagawikana. Pakutitu Asaduki anena kuti kulibe kuuka kwa akufa, kapena mngelo, kapena mzimu; koma Afarisi avomereza ponse pawiri. Ndipo chidauka chipolowe chachikulu, ndipo alembi ena a kwa Afarisi anaimirira, natsutsana, nanena, Sitipeza choipa chilichonse mwa munthuyu; ndipo nanga bwanji ngati mzimu kapena mngelo walankhula naye? Ndipo pamene padauka chipolowe chachikulu, kapitao wamkulu anaopa kuti angamkadzule Paulo, ndipo analamulira asilikali atsike, namkwatule pakati pao, nadze naye kulowa naye m'linga. Ndipo usiku wake Ambuye anaimirira pa iye, nati, Limbika mtima; pakuti monga wandichitira umboni ku Yerusalemu, koteronso uyenera kundichitira umboni ku Roma. Ndipo kutacha, Ayuda anapangana chiwembu, nadzitemberera, ndi kunena kuti sadzadya kapena kumwa kanthu, kufikira atamupha Paulo; ndipo iwo amene adachita chilumbiro ichi anali oposa makumi anai. Amenewo anadza kwa ansembe aakulu ndi akulu, nati, Tadzitemberera nalo temberero kuti sitidzalawa kanthu kufikira titamupha Paulo. Potero tsopano inu ndi bwalo la akulu muzindikiritse kapitao wamkulu kuti atsike naye kwa inu, monga ngati mufuna kudziwitsitsa bwino za iye; koma tadzikonzeratu timuphe asanayandikire iye. Koma mwana wa mlongo wake wa Paulo anamva za chifwamba chao, ndipo anadza nalowa m'linga, namfotokozera Paulo. Ndipo Paulo anadziitanira kenturiyo wina, nati, Pita naye mnyamata uyu kwa kapitao wamkulu; pakuti ali nako kanthu kakumfotokozera iye. Pamenepo ndipo anamtenga, napita naye kwa kapitao wamkulu, nati, Wam'nsingayo Paulo anandiitana, nandipempha ndidze naye mnyamata uyu kwa inu, ali nako kanthu kakulankhula ndi inu. Ndipo kapitao wamkulu anamgwira dzanja, napita naye padera, namfunsa m'tseri, Chiyani ichi uli nacho kundifotokozera? Ndipo anati, Ayuda anapangana kuti akufunseni mutsike naye Paulo mawa kubwalo la milandu, monga ngati mufuna kufunsitsa za iye. Pamenepo musakopedwe nao; pakuti amlalira iye oposa makumi anai a iwo amene anadzitemberera okha kuti sadzadya kapena kumwa kufikira atamupha iye; ndipo akonzekeratu tsopano nayang'anira lonjezano lanu. Pamenepo ndipo kapitao wamkulu anauza mnyamatayo apite, namlamulira kuti, Usauze munthu yense kuti wandizindikiritsa izi. Ndipo anaitana akenturiyo awiri, nati, Mukonzeretu asilikali mazana awiri, apite kufikira Kesareya, ndi apakavalo makumi asanu ndi awiri, ndi anthungo mazana awiri, achoke ora lachitatu la usiku; ndiponso mukonzeretu nyama zobereka amkwezepo Paulo, nampereke wosungika kwa Felikisi kazembeyo. Ndipo analembera kalata wakuti: Klaudio Lisiasi kwa kazembe womveketsa Felikisi, ndikupatsani moni. Munthu uyu anagwiridwa ndi Ayuda, ndipo akadaphedwa ndi iwo; pamenepo ndinafikako ine ndi asilikali, ndipo ndinamlanditsa pakumva kuti ndiye Mroma. Ndipo pofuna kuzindikira chifukwa chakuti anamnenera iye, ndinatsikira naye ku bwalo la akulu ao. Ndipo ndinapeza kuti adamnenera za mafunso a chilamulo chao; koma analibe kumnenera kanthu kakuyenera imfa kapena nsinga. Ndipo m'mene anandidziwitsa kuti pali chiwembu cha pa munthuyu, pomwepo ndinamtumiza kwa inu; ndipo ndalamulira akumnenera akamnenere kwa inu. Pamenepo ndipo asilikali, monga adawalamulira, anatenga Paulo, napita naye usiku ku Antipatri. Koma m'mawa mwake anasiya apakavalo amperekeze, nabwera kulinga; iwowo, m'mene anafika ku Kesareya, anapereka kalata kwa kazembe, naperekanso Paulo kwa iye. Ndipo m'mene adawerenga anafunsa achokera m'dziko liti; ndipo pozindikira kuti anali wa ku Silisiya, anati, Ndidzamva mlandu wako, pamene akukunenera afika. Ndipo analamulira kuti amdikire iye m'nyumba ya milandu ya Herode. Ndipo atapita masiku asanu anatsika mkulu wa ansembe Ananiya pamodzi ndi akulu ena, ndi wogwira moyo dzina lake Tertulo; ndipo anafotokozera kazembeyo za kunenera Paulo. Ndipo pamene adamuitana, Tertulo anayamba kumnenera ndi kunena, Popeza tili nao mtendere wambiri mwa inu, ndipo mwa kuganiziratu kwanu muukonzera mtundu wathu zotiipsa, tizilandira ndi chiyamiko chonse, monsemo ndi ponsepo, Felikisi womveka inu. Koma kuti ndingaonjeze kukulemetsani ndikupemphani mutimvere mwachidule ndi chifatso chanu. Pakuti tapeza munthuyu ali ngati mliri, ndi woutsa mapanduko kwa Ayuda onse m'dziko lonse lokhalamo anthu, ndi mtsogoleri wa mpanduko wa Anazarene; amenenso anayesa kuipsa Kachisi; amene tamgwira. *** Ndipo kwa iye mudzakhoza kuzindikira pomfunsa nokha, za izi zonse timnenerazi. Ndipo Ayudanso anavomerezana naye, natsimikiza kuti izi zitero. Ndipo pamene kazembe anamkodola kuti anene, Paulo anayankha, Podziwa ine kuti mwakhala woweruza wa mtundu uwu zaka zambiri, ndidzikanira mokondwera; popeza mukhoza kuzindikira kuti apita masiku khumi ndi awiri okha chikwerere ine ku Yerusalemu kukalambira; ndipo sanandipeza m'Kachisi wotsutsana ndi munthu, kapena kuutsa khamu la anthu, kapena m'sunagoge kapena m'mzinda. Ndipo sangathe kukutsimikizirani zimene andinenera ine tsopano. Koma ichi ndivomera kwa inu, kuti monga mwa Njira yonenedwa mpatuko, momwemo nditumikira Mulungu wa makolo athu, ndi kukhulupirira zonse zili monga mwa chilamulo, ndi zolembedwa mwa aneneri; ndi kukhala nacho chiyembekezo cha kwa Mulungu chimene iwo okhanso achilandira, kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama. M'menemonso ndidziyesera ndekha ndikhale nacho nthawi zonse chikumbu mtima chosanditsutsa cha kwa Mulungu ndi kwa anthu. Ndipo zitapita zaka zambiri ndinadza kutengera mtundu wanga zachifundo, ndi zopereka; popereka izi anandipeza woyeretsedwa m'Kachisi, wopanda khamu la anthu, kapena phokoso; koma panali Ayuda ena a ku Asiya, ndiwo mwenzi atakhala pano pamaso panu ndi kundinenera, ngati ali nako kanthu kotsutsa ine. Kapena iwo amene ali kunowa anene anapeza chosalungama chotani, poimirira ine pamaso pa bwalo la akulu, koma mau awa amodzi okha, amene ndinafuula poimirira pakati pao, Kunena za kuuka kwa akufa ndiweruzidwa ndi inu lero lino. Koma Felikisi anawalinditsa, popeza anadziwitsadi Njirayo, nati, Pamene Lisiasi kapitao wamkulu akatsika ndidzazindikiritsa konse za kwa inu. Ndipo analamulira kenturiyo amsunge iye, koma akhale nao ufulu, ndipo asaletse anthu ake kumtumikira. Koma atapita masiku ena, anadza Felikisi ndi Durusila mkazi wake, ndiye Myuda, naitana Paulo, ndipo anamva iye za chikhulupiriro cha Khristu Yesu. Ndipo m'mene anamfotokozera za chilungamo, ndi chidziletso, ndi chiweruziro chilinkudza, Felikisi anagwidwa ndi mantha, nayankha, Pita tsopano; ndipo ndikaona nthawi, ndidzakuitana iwe. Anayembekezanso kuti Paulo adzampatsa ndalama; chifukwa chakenso anamuitana iye kawirikawiri, nakamba naye. Koma zitapita zaka ziwiri Porkio Fesito analowa m'malo a Felikisi; ndipo Felikisi pofuna kukonda Ayuda anamsiya Paulo m'nsinga. Pamenepo Fesito m'mene analowa dziko lake, ndipo atapita masiku atatu, anakwera kunka ku Yerusalemu kuchokera ku Kesareya. Ndipo ansembe aakulu ndi akulu a Ayuda ananenera Paulo kwa iye; ndipo iwo anamdandaulira, nampempha kuti mlandu wake wa Paulo uipe, kuti amuitane iye adze ku Yerusalemu; iwo amchitira chifwamba kuti amuphe panjira. Pamenepo Fesito anayankha, kuti Paulo asungike ku Kesareya, ndi kuti iye mwini adzapitako posachedwa. Chifukwa chake, ati, iwo amene akhoza mwa inu amuke nane potsikirako, ndipo ngati kuli kanthu kosayenera mwa munthuyo amnenere iye. Ndipo m'mene adatsotsa mwa iwo masiku asanu ndi atatu kapena khumi okha anatsikira ku Kesareya; ndipo m'mawa mwake anakhala pa mpando wachiweruziro, nalamulira kuti atenge Paulo. Ndipo m'mene anafika iye, Ayuda adatsikawo ku Yerusalemu anaimirira pomzinga iye, namnenera zifukwa zambiri ndi zazikulu, zimene sanakhoza kuzitsimikiza; koma Paulo podzikanira ananena, Sindinachimwa kanthu kapena pachilamulo cha Chiyuda, kapena pa Kachisi, kapena pa Kaisara. Koma Fesito pofuna kuyesedwa wachisomo ndi Ayuda, anayankha kwa Paulo, nati, Kodi ufuna kukwera kunka ku Yerusalemu, ndi kuweruzidwa ndi ine pomwepo kunena za zinthu izi? Koma Paulo anati, Ndilikuimirira pa mpando wachiweruziro wa Kaisara, pompano ndiyenera kuweruzidwa ine; Ayuda sindinawachitira kanthu koipa, monga mudziwanso nokha bwino. Pamenepo ngati ndili wochita zoipa, ngati ndachita kanthu kakuyenera imfa, sindikana kufa; koma ngati zinthuzi awa andinenera nazo zili zachabe, palibe mmodzi akhoza kundipereka kwa iwo. Nditulukira kwa Kaisara. Pamenepo Fesito, atakamba ndi aphungu ake, anayankha, Wanena, Nditulukira kwa Kaisara; kwa Kaisara udzapita. Ndipo atapita masiku ena, Agripa mfumuyo, ndi Berenise anafika ku Kesareya, nalankhula Fesito. Ndipo atatsotsako masiku ambiri, Fesito anafotokozera mfumuyo mlandu wake wa Paulo, nanena, Pali munthu adamsiya m'ndende Felikisi, amene ansembe aakulu ndi akulu a Ayuda anamnenera kwa ine, ndili ku Yerusalemu, nandipempha ndiipitse mlandu wake. Koma ndinawayankha, kuti machitidwe a Aroma satero, kupereka munthu asanayambe woneneredwayo kupenyana nao omnenera ndi kukhala napo podzikanira pa chomneneracho. Potero, pamene adasonkhana pano, sindinachedwa, koma m'mawa mwake ndinakhala pa mpando wachiweruziro, ndipo ndinalamulira adze naye munthuyo. Ndipo pamene anaimirira omneneza, sanamtchulira konse chifukwa cha zoipa zonga ndinazilingirira ine; koma anali nao mafunso ena otsutsana naye a chipembedzero cha iwo okha, ndi mafunso a wina Yesu, amene adafa, amene Paulo anati kuti ali ndi moyo. Ndipo ine posinkhasinkha za mafunso awa ndinamfunsa ngati afuna kupita ku Yerusalemu, ndi kuweruzidwa komweko za izi. Koma pakunena Paulo ndi kuti, asungidwe, akatulukire kwa Augusto, ndinaweruza asungidwe iye kufikira ndikamtumiza kwa Kaisara. Ndipo Agripa anati kwa Fesito, Ndifuna nanenso ndimve munthuyo. Anati, Mawa mudzamva iye. M'mawa mwake tsono, atafika Agripa ndi Berenise ndi chifumu chachikulu, ndipo atalowa momvera milandu, pamodzi ndi akapitao akulu, ndi amuna omveka a mudziwo, ndipo pakulamulira Fesito, anadza naye Paulo. Ndipo Fesito anati, Mfumu Agripa, ndi amuna inu nonse muli nafe pano pamodzi, muona uyu, amene unyinji wonse wa Ayuda anandiuza za iye, ku Yerusalemu ndi kunonso, ndi kufuula kuti sayeneranso kukhala ndi moyo. Koma ndinapeza ine kuti sanachita kanthu koyenera imfa iye; ndipo popeza iye yekha anati akatulukire kwa Augusto, ndatsimikiza mtima kumtumizako. Koma ndilibe ine kanthu koti ndinenetse za iye kakulembera kwa mbuye wanga. Chifukwa chake ndamtulutsira kwa inu, ndipo makamaka kwa inu, Mfumu Agripa, kuti, ndikatha kumfunsafunsa, ndikhale nako kanthu kakulembera. Pakuti chindionekera chopanda nzeru, potumiza wam'nsinga, wosatchulanso zifukwa zoti amneneze. Ndipo Agripa anati kwa Paulo, Kwaloleka udzinenere wekha. Pamenepo Paulo, anatambasula dzanja nadzikanira: Ndidziyesera wamwai, Mfumu Agripa, popeza nditi ndidzikanira lero pamaso panu, za zonse zimene Ayuda andinenera nazo; makamaka popeza mudziwitsa miyambo yonse ndi mafunso onse a mwa Ayuda; chifukwa chake ndikupemphani mundimvere ine moleza mtima. Mayendedwe a moyo wanga tsono, kuyambira pa chibwana changa, amene anakhala chiyambire mwa mtundu wanga m'Yerusalemu, awadziwa Ayuda onse; andidziwa ine chiyambire, ngati afuna kuchitapo umboni, kuti ndinakhala Mfarisi monga mwa mpatuko wolunjikitsitsa wa chipembedzero chathu. Ndipo tsopano ndiimirira pano ndiweruzidwe pa chiyembekezo cha lonjezano limene Mulungu analichita kwa makolo athu; kufikira komweko mafuko athu khumi ndi awiri, potumikira Mulungu kosapumula usiku ndi usana, ayembekeza kufikirako. Chifukwa cha chiyembekezo ichi, Mfumu, andinenera Ayuda. Muchiyesa chinthu chosakhulupirika, chakuti Mulungu aukitsa akufa? Inedi ndinayesa ndekha, kuti kundiyenera kuchita zinthu zambiri zotsutsana nalo dzina la Yesu Mnazarayo. Chimenenso ndinachita m'Yerusalemu: ndipo ndinatsekera ine oyera mtima ambiri m'ndende, popeza ndidalandira ulamuliro wa kwa ansembe aakulu; ndiponso pophedwa iwo, ndinavomerezapo. Ndipo ndinawalanga kawirikawiri m'masunagoge onse, ndi kuwakakamiza anene zamwano; ndipo pakupsa mtima kwakukulu pa iwo ndinawalondalonda ndi kuwatsata ngakhale kufikira kumidzi yakunja. M'menemo popita ine ku Damasiko ndi ulamuliro ndi ukumu wa kwa ansembe aakulu, dzuwa lamsana, ndinaona panjira, Mfumu, kuunika kochokera kumwamba kowalitsa koposa dzuwa kunawala pondizinga ine ndi iwo akundiperekeza. Ndipo pamene tidagwa pansi tonse, ndinamva mau akunena kwa ine m'chinenedwe cha Chihebri, Saulo, Saulo, undilondalonderanji Ine? Nkukuvuta kutsalima pachotwikira. Ndipo ndinati, Ndinu yani Mbuye? Ndipo Ambuye anati, Ine ndine Yesu amene iwe umlondalonda. Komatu uka, imirira pa mapazi ako; pakuti chifukwa cha ichi ndinaonekera kwa iwe, kukuika iwe ukhale mtumiki ndi mboni ya izi wandionamo Ine, ndiponso ya izi ndidzakuonekeramo iwe; ndi kukulanditsa kwa anthu, ndi kwa amitundu, amene Ine ndikutuma kwa iwo, kukawatsegulira maso ao, kuti atembenuke kuchokera kumdima, kulinga kukuunika, ndi kuchokera ulamuliro wa Satana kulinga kwa Mulungu, kuti alandire iwo chikhululukiro cha machimo, ndi cholowa mwa iwo akuyeretsedwa ndi chikhulupiriro cha mwa Ine. Potero, Mfumu Agripa, sindinakhala ine wosamvera masomphenya a Kumwamba; komatu kuyambira kwa iwo a m'Damasiko, ndi a m'Yerusalemu, ndi m'dziko lonse la Yudeya, ndi kwa amitundunso ndinalalikira kuti alape, natembenukire kwa Mulungu, ndi kuchita ntchito zoyenera kutembenuka mtima. Chifukwa cha izi Ayuda anandigwira m'Kachisi, nayesa kundipha. Pamenepo pothandizidwa ndi Mulungu, ndiimirira kufikira lero lino, ndi kuwachitira umboni ang'ono ndi akulu, osanena kanthu kena koma zimene aneneri ndi Mose ananena zidzafika; kuti Khristu akamve zowawa, kuti Iye, woyamba mwa kuuka kwa akufa, adzalalikira kuunika kwa anthu ndi kwa amitundu. Koma pakudzikanira momwemo, Fesito anati ndi mau akulu, Uli wamisala Paulo; kuwerengetsa kwako kwakuchititsa misala. Koma Paulo anati, Ndilibe misala, Fesito womvekatu; koma nditulutsa mau a choonadi ndi odziletsa. Pakuti mfumuyo idziwa izi, kwa iye imene ndilankhula nayonso mosaopa: pakuti ndidziwadi kuti kulibe kanthu ka izi kadambisikira; pakuti ichi sichinachitika m'tseri. Mfumu Agripa, mukhulupirira aneneri kodi? Ndidziwa kuti muwakhulupirira. Ndipo Agripa anati kwa Paulo, Ndi kundikopa pang'ono ufuna kundiyesera mkhristu. Ndipo Paulo anati, Mwenzi atalola Mulungu, kuti ndi kukopa pang'ono, kapena ndi kukopa kwambiri, si inu nokha, komatunso onse akundimva ine lero, akadakhala otero onga ndili ine, osanena nsinga izi. Ndipo ananyamuka mfumu, ndi kazembe, ndi Berenise, ndi iwo akukhala nao; ndipo atapita padera analankhula wina ndi mnzake, nanena, Munthu uyu sanachita kanthu koyenera imfa, kapena nsinga. Ndipo Agripa anati kwa Fesito, Tikadakhoza kumasula munthuyu, akadapanda kunena, Ndikatulukire kwa Kaisara. Ndipo pamene padatsimikizika kuti tipite m'ngalawa kunka ku Italiya, anapereka Paulo ndi andende ena kwa kenturiyo dzina lake Julio, wa gulu la Augusto. Ndipo m'mene tidalowa m'ngalawa ya ku Adramitio ikati ipite kunka ku malo a ku mbali ya Asiya, tinakankha, ndipo Aristariko Mmasedoniya wa ku Tesalonika, anali nafe. Ndipo m'mawa mwake tinangokocheza ku Sidoni; ndipo Julio anachitira Paulo mwachikondi, namlola apite kwa abwenzi ake amchereze. Ndipo pokankhanso pamenepo, tinapita kuseri kwa Kipro, popeza mphepo inaomba mokomana nafe. Ndipo pamene tidapyola nyanja ya kunsi kwake kwa Silisiya ndi Pamfiliya, tinafika ku Mira wa Likiya. Ndipo kenturiyo anapezako ngalawa ya ku Aleksandriya, ilikupita ku Italiya, ndipo anatilongamo. Ndipo m'mene tidapita pang'onopang'ono masiku ambiri, ndi kufika movutika pandunji pa Kinido, ndipo popeza siinatilolanso mphepo, tinapita m'tseri mwa Krete, pandunji pa Salimone; ndipo popazapazapo movutika, tinafika kumalo ena dzina lake Pokocheza Pokoma; pafupi pamenepo panali mudzi wa Lasea. Ndipo itapita nthawi yambiri, ndipo unayambokhala woopsa ulendowo, popezanso nyengo ya kusala chakudya idapita kale, Paulo anawachenjeza, nanena nao, Amuna inu, ndiona ine kuti ulendo udzatitengera kuonongeka ndi kutayika kwambiri, si kwa akatundu okha kapena ngalawa yokha, komatunso kwa moyo wathu. Koma kenturiyo anakhulupirira watsigiro ndi mwini ngalawa makamaka, wosasamala mau a Paulo. Ndipo popeza dooko silinakoma kugonapo nyengo yachisanu, unyinji unachita uphungu ndi kuti amasule nachokepo, ngati kapena nkutheka afikire ku Fenikisi, ndi kugonako, ndilo dooko la ku Krete, loloza kumpoto ndi kumwera. Ndipo poomba pang'ono mwera, poyesa kuti anaona chofunirako, anakoka nangula, napita m'mbali mwa Krete. Koma patapita pang'ono idaombetsa kuchokerako mphepo ya namondwe, yonenedwa Yurakulo; ndipo pogwidwa nayo ngalawa, yosakhoza kupitanso mokomana nayo mphepo, tidangoleka, ndipo tinangotengedwa. Ndipo popita kuseri kwa chisumbu chaching'ono dzina lake Kauda, tinakhoza kumangitsa bwato koma movutika; ndipo m'mene adaukweza, anachita nazo zothandizira, nakulunga ngalawa; ndipo pakuopa kuti angatayike pa Siriti, anatsitsa matanga, natengedwa motero. Ndipo povutika kwakukulu ndi namondweyo, m'mawa mwake anayamba kutaya akatundu; ndipo tsiku lachitatu anataya ndi manja ao a iwo eni zipangizo za ngalawa. Ndipo m'mene dzuwa kapena nyenyezi sizinatiwalira masiku ambiri, ndipo namondwe wosati wamng'ono anatigwera, chiyembekezo chonse chakuti tipulumuke chidatichokera pomwepo. Ndipo pamene atakhala nthawi yaikulu osadya kanthu, Paulo anaimirira pakati pao, nati, Amuna inu, mukadamvera ine, osachoka ku Krete, osadzitengera kuonongeka ndi kutayika kumene. Koma tsopano ndikuchenjezani mulimbike mtima; pakuti sadzatayika wamoyo mmodzi mwa inu, koma ngalawa ndiyo. Pakuti anaimirira kwa ine usiku walero mngelo wa Mulungu amene ndili wake, amenenso ndimtumikira, nanena, Usaope Paulo; ukaimirira pamaso pa Kaisara; ndipo, taona, Mulungu anakupatsa onse amene akuyenda nawe pamodzi. Chifukwa chake, limbikani mtima, amuna inu; pakuti ndikhulupirira Mulungu, kuti kudzatero monga momwe ananena ndi ine. Koma tiyenera kutayika pa chisumbu chakuti. Koma pofika usiku wakhumi ndi chinai, potengedwa ife kwina ndi kwina m'nyanja ya Adriya, pakati pa usiku amalinyero anazindikira kuti analikuyandikira kumtunda; ndipo anayesa madzi, napeza mikwamba makumi awiri; ndipo katapita kanthawi, anayesanso, napeza mikwamba khumi ndi isanu. Ndipo pakuopa tingatayike pamiyala, anaponya anangula anai kumakaliro, nakhumba kuti kuche. Ndipo m'mene amalinyero anafuna kuthawa m'ngalawa, natsitsira bwato m'nyanja, monga ngati anati aponye anangula kulikulu, Paulo anati kwa kenturiyo ndi kwa asilikali, Ngati awa sakhala m'ngalawa inu simukhoza kupulumuka. Pamenepo asilikali anadula zingwe za bwato, naligwetsa. Ndipo popeza kulinkucha, Paulo anawachenjeza onse adye kanthu, nati, Lero ndilo tsiku lakhumi ndi chinai limene munalindira, ndi kusala chakudya, osalawa kanthu. Momwemo ndikuchenjezani mutenge kanthu kakudya; pakuti kumeneku ndi kwa chipulumutso chanu; pakuti silidzatayika tsitsi la pa mutu wa mmodzi wa inu. Ndipo atanena izi, ndi kutenga mkate, anayamika Mulungu pamaso pa onse; ndipo m'mene adaunyema anayamba kudya. Ndipo anakhala olimbika mtima onse, natenga chakudya iwo omwe. Ndipo ife tonse tili m'ngalawa ndife anthu mazana awiri mphambu makumi asanu ndi awiri kudza asanu ndi mmodzi. Ndipo m'mene anakhuta, anapepuza ngalawa, nataya tirigu m'nyanja. Ndipo kutacha sanazindikira dzikolo; koma anaona pali bondo la mchenga; kumeneko anafuna, ngati nkutheka, kuyendetsako ngalawa. Ndipo m'mene anataya anangula anawasiya m'nyanja, namasulanso zingwe zomanga tsigiro; ndipo pokweza thanga la kulikulu, analunjikitsa kumchenga. Koma pofika pamalo pokomana mafunde awiri, anatsamitsapo ngalawa; ndipo kulikulu kunatsama, ndi kukhala kosasunthika, koma kumakaliro kunasweka ndi mphamvu ya mafunde. Ndipo uphungu wa asilikali udati awaphe andende, angasambire, ndi kuthawa. Koma kenturiyo, pofuna kupulumutsa Paulo, anawaletsa angachite cha uphungu wao; nalamula kuti iwo akukhoza kusambira ayambe kudziponya m'nyanja, nafike pamtunda, ndipo otsalawo, ena pamatabwa, ndi ena pa zina za m'ngalawa. Ndipo kudatero kuti onse adapulumukira pamtunda. Ndipo titapulumuka, pamenepo tinadziwa kuti chisumbucho chinatchedwa Melita. Ndipo akunja anatichitira zokoma zosachitika pena ponsepo; pakuti anasonkha moto, natilandira ife tonse, chifukwa cha mvula inalinkugwa, ndi chifukwa cha chisanu. Koma pamene Paulo adaola chisakata cha nkhuni, nachiika pamoto, inatulukamo njoka, chifukwa cha kutenthaku, niluma dzanja lake. Koma pamene akunjawo anaona chilombocho chili lende pa dzanja lake, ananena wina ndi mnzake, Zoona munthuyu ndiye wambanda. Angakhale anapulumuka m'nyanja, chilungamo sichimlola akhale ndi moyo. Koma anakutumulira chilombocho kumoto, osamva kupweteka. Koma anayesa kuti adzatupa, kapena mwini wake kugwa kufa pomwepo; koma m'mene adalindira nthawitu, naona kuti sikunampweteka, anapindula, nati, Ndiye Mulungu. Koma pafupi pamenepo panali minda, mwini wake ndiye mkulu chisumbucho, dzina lake Publio; amene anatilandira ife, natichereza okoma masiku atatu. Ndipo kunatero kuti atate wake wa Publioyo anagona wodwala nthenda ya malungo ndi kamwazi. Kwa iyeyu Paulo analowa, napemphera, naika manja pa iye, namchiritsa. Ndipo patachitika ichi, enanso a m'chisumbu, okhala nazo nthenda, anadza, nachiritsidwa; amenenso anatichitira ulemu wambiri; ndipo pochoka ife anatiikira zotisowa. Ndipo itapita miyezi itatu tinayenda m'ngalawa ya ku Aleksandriya, idagonera nyengo ya chisanu kuchisumbuko, chizindikiro chake, Ana Amapasa. Ndipo pamene tinakocheza ku Sirakusa, tinatsotsako masiku atatu. Ndipo pochokapo tinapaza ntifika ku Regio; ndipo litapita tsiku limodzi unayamba mwera, ndipo m'mawa mwake tinafika ku Puteoli: pamenepo tinakomana ndi abale, amene anatiumirira tikhale nao masiku asanu ndi awiri; ndipo potero tinafika ku Roma. Kuchokera kumeneko abalewo, pakumva za ife, anadza kukomana nafe ku Bwalo la Apio, ndi ku Nyumba za Alendo Zitatu; ndipo pamene Paulo anawaona, anayamika Mulungu, nalimbika mtima. Ndipo pamene tinalowa m'Roma, analola Paulo akhale pa yekha ndi msilikali womdikira iye. Ndipo kunali, atapita masiku atatu, anaitana akulu a Ayuda asonkhane; ndipo atasonkhana, ananena nao, Ine, amuna, abale, ndingakhale sindinachita kanthu kakuipsa anthu, kapena miyambo ya makolo, anandipereka wam'nsinga kuchokera ku Yerusalemu ku manja a Aroma; ndiwo, atandifunsafunsa ine anafuna kundimasula, popeza panalibe chifukwa cha kundiphera. Koma pakukanapo Ayuda, ndinafulumidwa mtima kutulukira kwa Kaisara; si kunena kuti ndinali nako kanthu kakunenera mtundu wanga. Chifukwa cha ichi tsono ndinakupemphani inu mundione ndi kulankhula nane; pakuti chifukwa cha chiyembekezo cha Israele ndamangidwa ndi unyolo uwu. Ndipo anati kwa iye, Ife sitinalandira akalata onena za inu ochokera ku Yudeya, kapena sanadza kuno wina wa abale ndi kutiuza kapena kulankhula kanthu koipa ka inu. Koma tifuna kumva mutiuze muganiza chiyani; pakuti za mpatuko uwu, tidziwa kuti aunenera ponseponse. Ndipo pamene adampangira tsiku, anadza kunyumba yake anthu ambiri; amenewo anawafotokozera, ndi kuchitira umboni Ufumu wa Mulungu, ndi kuwakopa za Yesu, zochokera m'chilamulo cha Mose ndi mwa aneneri, kuyambira mamawa kufikira madzulo. Ndipo ena anamvera zonenedwazo, koma ena sanamvere. Koma popeza sanavomerezana, anachoka atanena Paulo mau amodzi, kuti, Mzimu Woyera analankhula kokoma mwa Yesaya Mneneri kwa makolo anu, ndi kuti, Pita kwa anthu awa, nuti, Ndi kumva mudzamva, ndipo simudzazindikira konse; ndipo pakupenya mudzapenya, koma osaona konse; pakuti mtima wa anthu awa watupatu, ndipo m'makutu mwao mmolema kumva, ndipo maso ao anawatseka; kuti angaone ndi maso, nangamve ndi makutu, nangazindikire ndi mtima, nangatembenuke, ndipo Ine ndingawachiritse. Potero, dziwani inu, kuti chipulumutso ichi cha Mulungu chitumidwa kwa amitundu; iwonso adzamva. *** Ndipo anakhala zaka ziwiri zamphumphu m'nyumba yake yobwereka, nalandira onse akufika kwa iye, ndi kulalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuphunzitsa za Ambuye Yesu Khristu ndi kulimbika konse, wosamletsa munthu. Paulo, kapolo wa Yesu Khristu, mtumwi woitanidwa, wopatulidwa kukanena Uthenga Wabwino wa Mulungu, umene Iye analonjeza kale ndi mau a aneneri ake m'malembo oyera, wakunena za Mwana wake, amene anabadwa, wa mbeu ya Davide, monga mwa thupi, amene anatsimikizidwa ndi mphamvu kuti ndiye Mwana wa Mulungu monga mwa Mzimu wa chiyero, ndi kuuka kwa akufa; ndiye Yesu Khristu Ambuye wathu; amene ife tinalandira naye chisomo ndi utumwi, kuti amvere chikhulupiriro anthu a mitundu yonse chifukwa cha dzina lake; mwa amenewo muli inunso, oitanidwa a Yesu Khristu; kwa onse a ku Roma, okondedwa a Mulungu, oitanidwa kuti akhale oyera mtima: Chisomo chikhale ndinu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu. Poyamba, ndiyamika Mulungu wanga mwa Yesu Khristu chifukwa cha inu nonse, chifukwa kuti mbiri ya chikhulupiriro chanu idamveka pa dziko lonse lapansi. Pakuti Mulungu ali mboni yanga, amene ndimtumikira mu mzimu wanga, m'Uthenga Wabwino wa Mwana wake, kuti kosalekeza ndikumbukira inu, ndi kupempha masiku onse m'mapemphero anga, ngati nkutheka tsopano mwa chifuniro cha Mulungu, ndione ulendo wabwino, wakudza kwa inu. Pakuti ndilakalaka kuonana ndinu, kuti ndikagawire kwa inu mtulo wina wauzimu, kuti inu mukhazikike; ndiko, kuti ine ndikatonthozedwe pamodzi ndi inu, mwa chikhulupiriro cha ife tonse awiri, chanu ndi changa. Ndipo sindifuna kuti inu, abale, mudzakhala osadziwa, kuti kawirikawiri ndikanena mumtima kuti ndikafike kwa inu, koma ndaletsedwa kufikira lero, kuti ndikaone zobala zina mwa inunso, monga mwa anthu amitundu ena. Ine ndili wamangawa wa Agriki ndi wa akunja, wa anzeru ndi wa opusa. Chotero, momwe ndingakhoze ine, ndilikufuna kulalikira Uthenga Wabwino kwa inunso a ku Roma. Pakuti Uthenga Wabwino sundichititsa manyazi; pakuti uli mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa munthu aliyense wakukhulupirira; kuyambira Myuda, ndiponso Mgriki. Pakuti m'menemo chaonetsedwa chilungamo cha Mulungu chakuchokera kuchikhulupiriro kuloza kuchikhulupiriro: monga kwalembedwa, Koma munthu wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhulupiriro. Pakuti mkwiyo wa Mulungu, wochokera Kumwamba, uonekera pa chisapembedzo chonse ndi chosalungama cha anthu, amene akanikiza pansi choonadi m'chosalungama chao; chifukwa chodziwika cha Mulungu chaonekera m'kati mwao; pakuti Mulungu anachionetsera kwa iwo. Pakuti chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mau akuwiringula; chifukwa kuti, ngakhale anadziwa Mulungu, sanamchitira ulemu wakuyenera Mulungu, ndipo sanamyamika; koma anakhala opanda pake m'maganizo ao, ndipo unada mtima wao wopulukira. Pakunena kuti ali anzeru, anapusa; nasandutsa ulemerero wa Mulungu wosaonongeka, naufanizitsa ndi chifaniziro cha munthu woonongeka ndi cha mbalame, ndi cha nyama zoyendayenda, ndi cha zokwawa. Chifukwa chake Mulungu anawapereka iwo m'zilakolako za mitima yao, kuzonyansa, kuchititsana matupi ao wina ndi mnzake zamanyazi; amenewo anasandutsa choonadi cha Mulungu chabodza napembedza, natumikira cholengedwa, ndi kusiya Wolengayo, ndiye wolemekezeka nthawi yosatha. Amen. Chifukwa cha ichi Mulungu anawapereka iwo ku zilakolako za manyazi: pakuti angakhale akazi ao anasandutsa machitidwe ao a chibadwidwe akhale machitidwe osalingana ndi chibadwidwe: ndipo chimodzimodzinso amuna anasiya machitidwe a chibadwidwe cha akazi, natenthetsana ndi cholakalaka chao wina ndi mnzake, amuna okhaokha anachitirana chamanyazi, ndipo analandira mwa iwo okha mphotho yakuyenera kulakwa kwao. Ndipo monga iwo anakana kukhala naye Mulungu m'chidziwitso chao, anawapereka Mulungu kumtima wokanika, kukachita zinthu zosayenera; anadzala ndi zosalungama zonse, kuipa, kusirira, dumbo; odzala ndi kaduka, mbanda, ndeu, chinyengo, udani; akazitape, osinjirira, akumuda Mulungu, achipongwe, odzitama, amatukutuku, oyamba zoipa, osamvera akulu ao, opanda nzeru, osasunga mapangano, opanda chikondi cha chibadwidwe, opanda chifundo; amene ngakhale adziwa kuweruza kwake kwa Mulungu, kuti iwo amene achita zotere ayenera imfa, azichita iwo okha, ndiponso avomerezana ndi iwo akuzichita. Chifukwa chake uli wopanda mau owiringula, munthu iwe, amene uli yense wakuweruza; pakuti m'mene uweruza wina, momwemo udzitsutsa iwe wekha, pakuti iwe wakuweruza, umachita zomwezo. Ndipo tidziwa kuti kuweruza kwa Mulungu kuli koona pa iwo akuchita zotere. Ndipo uganiza kodi, munthu iwe, amene umaweruza iwo akuchita zotere, ndipo uzichitanso iwe mwini, kuti udzapulumuka pa mlandu wa Mulungu? Kapena upeputsa kodi kulemera kwa ubwino wake, ndi chilekerero ndi chipiriro chake, wosadziwa kuti ubwino wa Mulungu ukubwezera kuti ulape? Koma kolingana ndi kuuma kwako, ndi mtima wako wosalapa, ulikudziunjikira wekha mkwiyo pa tsiku la mkwiyo ndi la kuvumbulutsa kuweruza kolungama kwa Mulungu; amene adzabwezera munthu aliyense kolingana ndi ntchito zake; kwa iwo amene afunafuna ulemerero ndi ulemu ndi chisaonongeko, mwa kupirira pa ntchito zabwino, adzabwezera moyo wosatha; koma kwa iwo andeu, ndi osamvera choonadi, koma amvera chosalungama, adzabwezera mkwiyo ndi kuzaza, nsautso ndi kuwawa mtima, kwa moyo wa munthu aliyense wakuchita zoipa, kuyambira Myuda, komanso Mgriki; koma ulemerero ndi ulemu ndi mtendere kwa munthu aliyense wakuchita zabwino, kuyambira Myuda, ndiponso Mgriki; pakuti Mulungu alibe tsankho. Pakuti onse amene anachimwa opanda lamulo adzaonongeka opanda lamulo; ndi onse amene anachimwa podziwa lamulo adzaweruzidwa ndi lamulo; pakuti akumvaimva lamulo sakhala olungama pamaso pa Mulungu, koma akuchita lamulo adzayesedwa olungama. Pakuti pamene anthu a mitundu akukhala opanda lamulo, amachita mwa okha za lamulo, omwewo angakhale alibe lamulo, adzikhalira okha ngati lamulo; popeza iwo aonetsa ntchito ya lamulolo yolembedwa m'mitima yao, ndipo chikumbu mtima chao chichitiranso umboni pamodzi nao, ndipo maganizo ao wina ndi mnzake anenezana kapena akanirana; tsiku limene Mulungu adzaweruza ndi Khristu Yesu zinsinsi za anthu, monga mwa Uthenga wanga Wabwino. Koma ngati iwe unenedwa Myuda, nukhazikika palamulo, nudzitamandira pa Mulungu, nudziwa chifuniro chake, nuvomereza zinthu zoposa, utaphunzitsidwa m'chilamulo, nulimbika mumtima kuti iwe wekha uli wotsogolera wa akhungu, nyali ya amene akhala mumdima, wolangiza wa opanda nzeru, mphunzitsi wa tiana, wakukhala m'chilamulo ndi chionekedwe cha nzeru ndi cha choonadi; ndiwe tsono wakuphunzitsa wina, kodi ulibe kudziphunzitsa mwini? Iwe wakulalikira kuti munthu asabe, kodi ulikuba mwini wekha? Iwe wakunena kuti munthu asachite chigololo, kodi umachita chigololo mwini wekha? Iwe wakudana nao mafano, umafunkha za m'Kachisi kodi? Iwe wakudzitamandira pachilamulo, kodi uchitira Mulungu mwano ndi kulakwa kwako m'chilamulo? Pakuti dzina la Mulungu lichitidwa mwano chifukwa cha inu, pakati pa anthu a mitundu, monga mwalembedwa. Pakuti inde mdulidwe uli wabwino, ngati iwe umachita lamulo; koma ngati uli wolakwira lamulo, mdulidwe wako wasanduka kusadulidwa. Chifukwa chake ngati wosadulidwa asunga zoikika za chilamulo, kodi kusadulidwa kwake sikudzayesedwa ngati mdulidwe? Ndipo kusadulidwa, kumene kuli kwa chibadwidwe, ngati kukwanira chilamulo, kodi sikudzatsutsa iwe, amene uli nao malembo ndi mdulidwe womwe, ndiwe wolakwira lamulo? Pakuti siali Myuda amene akhala wotere pamaso, kapena suli mdulidwe umene uli wotere pamaso, m'thupimo; koma Myuda ndiye amene akhala wotere mumtima; ndipo mdulidwe uli wa mtima, mumzimu, si m'malembo ai; kuyamika kwake sikuchokera kwa anthu, koma kwa Mulungu. Ndipo potero Myuda aposa ninji? Kapena mdulidwe upindulanji? Zambiri monsemonse: choyamba, kuti mau a Mulungu anaperekedwa kwa iwo. Nanga bwanji ngati ena sanakhulupirira? Kodi kusakhulupirira kwao kuyesa chabe chikhulupiriko cha Mulungu? Msatero ai. Koma Mulungu akhale woona, ndimo anthu onse akhale onama; monga kwalembedwa, Kuti Inu mukayesedwe wolungama m'maneno anu, ndi kuti mukalakike m'mene muweruzidwa. Koma ngati chosalungama chathu chitsimikiza chilungamo cha Mulungu, tidzatani ife? Kodi ali wosalungama Mulungu, amene afikitsa mkwiyo? (Ndilankhula umo anenera munthu). Msatero ai. Ngati kotero, Mulungu adzaweruza bwanji mlandu wa dziko lapansi? Pakuti ngati choonadi cha Mulungu chichulukitsa ulemerero wake chifukwa cha bodza langa, nanga inenso ndiweruzidwa bwanji monga wochimwa? Ndipo tilekerenji kunena, Tichite zoipa kuti zabwino zikadze (monganso ena atinamiza ndi kuti timanena)? Kulanga kwa amenewo kuli kolungama. Ndipo chiyani tsono? Kodi tiposa ife? Iai ndithu; pakuti tidawaneneza kale Ayuda ndi Agriki omwe, kuti onsewa agwidwa ndi uchimo; monga kwalembedwa, Palibe mmodzi wolungama, inde palibe mmodzi; palibe mmodzi wakudziwitsa, palibe mmodzi wakulondola Mulungu; onsewa apatuka, pamodzi akhala opanda pake; palibe mmodzi wakuchita zabwino, inde, palibe mmodzi ndithu. M'mero mwao muli manda apululu; ndi lilime lao amanyenga; ululu wa mamba uli pansi pa milomo yao; m'kamwa mwao mudzala ndi zotemberera ndi zowawa; miyendo yao ichita liwiro kukhetsa mwazi; kusakaza ndi kusauka kuli m'njira zao; ndipo njira ya mtendere sanaidziwa; kumuopa Mulungu kulibe pamaso pao. Ndipo tidziwa kuti zinthu zilizonse chizinena chilamulo chizilankhulira iwo ali nacho chilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi litsutsidwe ndi Mulungu; chifukwa kuti pamaso pake palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi ntchito za lamulo; pakuti uchimo udziwika ndi lamulo. Koma tsopano chilungamo cha Mulungu chaoneka chopanda lamulo, chilamulo ndi aneneri achitira ichi umboni; ndicho chilungamo cha Mulungu chimene chichokera mwa chikhulupiriro cha pa Yesu Khristu kwa onse amene akhulupirira; pakuti palibe kusiyana; pakuti onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu; ndipo ayesedwa olungama kwaulere, ndi chisomo chake, mwa chiombolo cha mwa Khristu Yesu; amene Mulungu anamuika poyera akhale chotetezera mwa chikhulupiriro cha m'mwazi wake, kuti aonetse chilungamo chake, popeza Mulungu m'kulekerera kwake analekerera machimo ochitidwa kale lomwe; kuti aonetse chilungamo chake m'nyengo yatsopano; kuti Iye akhale wolungama, ndi wakumuyesa wolungama iye amene akhulupirira Yesu. Pamenepo kudzitama kuli kuti? Kwaletsedwa. Ndi lamulo lotani? La ntchito kodi? Iai; koma ndi lamulo la chikhulupiriro. Pakuti timuyesa munthu wolungama chifukwa cha chikhulupiriro, wopanda ntchito za lamulo. Kapena Mulungu ndiye wa Ayuda okhaokha kodi? Si wao wa amitundunso kodi? Eya, wa amitundunso: ngatitu ndiye Mulungu mmodzi, amene adzawayesa amdulidwe olungama ndi chikhulupiriro, ndi akusadulidwa mwa chikhulupiriro. Potero kodi lamulo tiyesa chabe mwa chikhulupiriro? Msatero ai; koma tikhazikitsa lamulo. Ndipo tsono tidzanena kuti Abrahamu, kholo lathu monga mwa thupi, analandira chiyani? Pakuti ngati Abrahamu anayesedwa wolungama chifukwa cha ntchito, iye akhala nacho chodzitamandira; koma kulinga kwa Mulungu ai. Pakuti lembo litani? Ndipo Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo chinawerengedwa kwa iye chilungamo. Ndipo kwa iye amene agwira ntchito, mphotho siiwerengedwa ya chisomo koma ya mangawa. Koma kwa iye amene sachita, koma akhulupirira Iye amene ayesa osapembedza ngati olungama, chikhulupiriro chake chiwerengedwa chilungamo. Monganso Davide anena za mdalitso wake wa munthu, amene Mulungu amwerengera chilungamo chopanda ntchito, ndi kuti, Odala iwo amene akhululukidwa kusaweruzika kwao, nakwiriridwa machimo ao. Wodala munthu amene Mulungu samwerengera uchimo. Mdalitso umenewu tsono uli kwa odulidwa kodi, kapena kwa osadulidwa omwe? Pakuti timati, Chikhulupiriro chake chinawerengedwa kwa Abrahamu chilungamo. Tsono chinawerengedwa bwanji? M'mene iye anali wodulidwa kapena wosadulidwa? Si wodulidwa ai, koma wosadulidwa; iye ndipo analandira chizindikiro cha mdulidwe, ndicho chosindikiza chilungamo cha chikhulupiriro, chomwe iye anali nacho asanadulidwe; kuti kotero iye akhale kholo la onse akukhulupirira, angakhale iwo sanadulidwa, kuti chilungamo chiwerengedwe kwa iwonso; ndiponso kholo la mdulidwe wa iwo amene siali a mdulidwe okha, koma wa iwo amene atsata mayendedwe a chikhulupiriro chija cha kholo lathu Abrahamu, chimene iye anali nacho asanadulidwe. Pakuti lonjezo lakuti iye adzakhala wolowa nyumba wa dziko lapansi silinapatsidwa kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake mwa lamulo, koma mwa chilungamo cha chikhulupiriro. Pakuti ngati iwo a lamulo akhala olowa nyumba, pamenepo chikhulupiriro chayesedwa chabe, ndimo lonjezo layesedwa lopanda pake; pakuti chilamulo chichitira mkwiyo; koma pamene palibe lamulo, pamenepo palibe kulakwa. Chifukwa chake chilungamo chichokera m'chikhulupiriro, kuti chikhale monga mwa chisomo; kuti lonjezo likhale lokhazikika kwa mbeu zonse; si kwa iwo a chilamulo okhaokha, koma kwa iwonso a chikhulupiriro cha Abrahamu; ndiye kholo la ife tonse; monga kwalembedwa: Ndinakukhazika iwe kholo la mitundu yambiri ya anthu pamaso pa Mulungu amene iye anamkhulupirira, amene apatsa akufa moyo, ndi kuitana zinthu zoti palibe, monga ngati zilipo. Amene anakhulupirira nayembekeza zosayembekezeka, kuti iye akakhale kholo la mitundu yambiri ya anthu, monga mwa chonenedwachi, Mbeu yako idzakhala yotere. Ndipo iye osafooka m'chikhulupiriro sanalabadira thupi lake, ndilo longa ngati lakufa pamenepo, (pokhala iye ngati zaka makumi khumi), ndi mimba ya Sara idaumanso; ndipo poyang'anira lonjezo la Mulungu sanagwedezeka chifukwa cha kusakhulupirira, koma analimbika m'chikhulupiriro, napatsa Mulungu ulemu, nakhazikikanso mumtima kuti, chimene Iye analonjeza, anali nayonso mphamvu yakuchichita. Chifukwa chake ichi chinawerengedwa kwa iye chilungamo. Ndipo ichi sichinalembedwa chifukwa cha iye yekhayekha, kuti chidawerengedwa kwa iye; koma chifukwa cha ifenso, kwa ife amene chidzawerengedwa kwa ife amene tikhulupirira Iye amene anaukitsa kwa akufa Yesu Ambuye wathu, amene anaperekedwa chifukwa cha zolakwa zathu, naukitsidwa chifukwa cha kutiyesa ife olungama. Popeza tsono tayesedwa olungama ndi chikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu; amene ife tikhoza kulowa naye ndi chikhulupiriro m'chisomo ichi m'mene tilikuimamo; ndipo tikondwera m'chiyembekezo cha ulemerero wa Mulungu. Ndipo si chotero chokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizolowezi; ndi chizolowezi chichita chiyembekezo: ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu Woyera, amene wapatsidwa kwa ife. Pakuti pamene tinali chikhalire ofooka, pa nyengo yake Khristu anawafera osapembedza. Pakuti ndi chivuto munthu adzafera wina wolungama; pakuti kapena wina adzalimbika mtima kufera munthu wabwino. Koma Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha m'menemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Khristu adatifera ife. Ndipo tsono popeza tinayesedwa olungama ndi mwazi wake, makamaka ndithu tidzapulumuka mkwiyo wa Mulungu mwa Iyeyo. Pakuti ngati, pokhala ife adani ake, tinayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wake, makamaka ndithu, popeza ife tayanjanitsidwa, tidzapulumuka ndi moyo wake. Ndipo si chotero chokha, koma ife tikondwera ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene talandira naye tsopano chiyanjanitso. Chifukwa chake, monga uchimo unalowa m'dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa. Pakuti kufikira nthawi ya lamulo uchimo unali m'dziko lapansi; koma uchimo suwerengedwa popanda lamulo. Komatu imfa inachita ufumu kuyambira kwa Adamu kufikira kwa Mose, ngakhale pa iwonso amene sanachimwa monga machimwidwe ake a Adamu, ndiye fanizo la wakudzayo. Koma mphatso yaulere siilingana ndi kulakwa. Pakuti ngati ambiriwo anafa chifukwa cha kulakwa kwa mmodziyo, makamaka ndithu chisomo cha Mulungu, ndi mphatso yaulere zakuchokera ndi munthu mmodziyo Yesu Khristu, zinachulukira anthu ambiri. Ndipo mphatso siinadza monga mwa mmodzi wakuchimwa, pakuti mlandu ndithu unachokera kwa munthu mmodzi kufikira kutitsutsa, koma mphatso yaulere ichokera ku zolakwa zambiri kufikira kutiyesa olungama. Pakuti ngati, ndi kulakwa kwa mmodzi, imfa inachita ufumu mwa mmodziyo; makamaka ndithu amene akulandira kuchuluka kwake kwa chisomo ndi kwa mphatso ya chilungamo, adzachita ufumu m'moyo mwa mmodzi, ndiye Yesu Khristu. Chifukwa chake, monga mwa kulakwa kumodzi kutsutsa kunafikira anthu onse; chomwechonso mwa chilungamitso chimodzi chilungamo cha moyo chinafikira anthu onse. Pakuti monga ndi kusamvera kwa munthu mmodzi ambiri anayesedwa ochimwa, chomwecho ndi kumvera kwa mmodzi ambiri adzayesedwa olungama. Ndipo lamulo linalowa moonjezera, kuti kulakwa kukachuluke; koma pamene uchimo unachuluka, pomwepo chisomo chinachuluka koposa; kuti, monga uchimo unachita ufumu muimfa, chomwechonso chisomo chikachite ufumu mwa chilungamo, kufikira moyo wosatha mwa Yesu Khristu Ambuye wathu. Chifukwa chake tidzatani? Tidzakhalabe m'uchimo kodi, kuti chisomo chichuluke? Msatero ai. Ife amene tili akufa ku uchimo, tidzakhala bwanji chikhalire m'menemo? Kapena kodi simudziwa kuti ife tonse amene tinabatizidwa mwa Khristu Yesu; tinabatizidwa mu imfa yake? Chifukwa chake tinaikidwa m'manda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo kulowa muimfa; kuti monga Khristu anaukitsidwa kwa akufa mwa ulemerero wa Atate, chotero ifenso tikayende m'moyo watsopano. Pakuti ngati ife tinakhala olumikizidwa ndi Iye m'chifanizidwe cha imfa yake, koteronso tidzakhala m'chifanizidwe cha kuuka kwake; podziwa ichi, kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa pamodzi ndi Iye, kuti thupilo la uchimo likaonongedwe, kuti ife tisakhalenso akapolo a uchimo; pakuti iye amene anafa anamasulidwa kuuchimo. Koma ngati ife tinafa ndi Khristu, tikhulupirira kuti tidzakhalanso amoyo ndi Iye; podziwa kuti Khristu anaukitsidwa kwa akufa, sadzafanso; imfa siichitanso ufumu pa Iye. Pakuti pakufa Iye, atafa ku uchimo kamodzi; ndipo pakukhala Iye wamoyo, akhala wamoyo kwa Mulungu. Chotero inunso mudziwerengere inu nokha ofafa ku uchimo, koma amoyo kwa Mulungu mwa Khristu Yesu. Chifukwa chake musamalola uchimo uchite ufumu m'thupi lanu la imfa kumvera zofuna zake: ndipo musapereke ziwalo zanu kuuchimo, zikhale zida za chosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo atatuluka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za chilungamo. Pakuti uchimo sudzachita ufumu pa inu; popeza simuli a lamulo koma a chisomo. Ndipo chiyani tsono? Tidzachimwa kodi chifukwa sitili a lamulo, koma a chisomo? Msatero ai. Kodi simudziwa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala akapolo ake akumvera iye, mukhalatu akapolo ake a yemweyo mulikumvera iye; kapena a uchimo kulinga kuimfa, kapena a umvero kulinga kuchilungamo? Koma ayamikidwe Mulungu, kuti ngakhale mudakhala akapolo a uchimo, tsopano mwamvera ndi mtima makhalidwe aja a chiphunzitso chimene munaperekedweracho; ndipo pamene munamasulidwa kuuchimo, munakhala akapolo a chilungamo. Ndilankhula manenedwe a anthu, chifukwa cha kufooka kwa thupi lanu; pakuti monga inu munapereka ziwalo zanu zikhale akapolo a chonyansa ndi a kusaweruzika kuti zichite kusaweruzika, inde kotero tsopano perekani ziwalo zanu zikhale akapolo a chilungamo kuti zichite chiyeretso. Pakuti pamene inu munali akapolo a uchimo, munali osatumikira chilungamo. Ndipo munali nazo zobala zanji nthawi ija, m'zinthu zimene muchita nazo manyazi tsopano? Pakuti chimaliziro cha zinthu izi chili imfa. Koma tsopano, pamene munamasulidwa kuuchimo, ndi kukhala akapolo a Mulungu, muli nacho chobala chanu chakufikira chiyeretso, ndi chimaliziro chake moyo wosatha. Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Khristu Yesu Ambuye wathu. Nanga kodi simudziwa, abale, pakuti ndilankhula ndi anthu akudziwa lamulo, kuti lamulolo lichita ufumu pa munthu nthawi zonse iye ali wamoyo? Pakuti mkazi wokwatidwa amangidwa ndi lamulo kwa mwamuna wake wamoyo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamulo la mwamunayo. Ndipo chifukwa chake, ngati iye akwatiwa ndi mwamuna wina, pokhala mwamuna wake wamoyo, adzanenedwa mkazi wachigololo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamuloli; chotero sakhala wachigololo ngati akwatiwa ndi mwamuna wina. Chotero, abale anga, inunso munayesedwa akufa ku chilamulo ndi thupi la Khristu; kuti mukakhale ake a wina, ndiye amene anaukitsidwa kwa akufa, kuti ife timbalire Mulungu zipatso. Pakuti pamene tinali m'thupi, zilakolako za machimo, zimene zinali mwa chilamulo, zinalikuchita m'ziwalo zathu, kuti zibalire imfa zipatso. Koma tsopano tinamasulidwa kuchilamulo, popeza tinafa kwa ichi chimene tinagwidwa nacho kale; chotero kuti titumikire mu mzimu watsopano, si m'chilembo chakale ai. Pamenepo tidzatani? Kodi chilamulo chili uchimo? Msatero ai. Koma ine sindikadazindikira uchimo, koma mwa lamulo ndimo; pakuti sindikadazindikira chilakolako sichikadati chilamulo, Usasirire; koma uchimo, pamene unapeza chifukwa, unachita m'kati mwanga zilakolako zonse mwa lamulo; pakuti popanda lamulo uchimo uli wakufa. Ndipo kale ine ndinali wamoyo popanda lamulo; koma pamene lamulo linadza, uchimo unatsitsimuka, ndipo ine ndinafa. Ndipo lamulo, limene linali lakupatsa moyo, ndinalipeza lakupatsa imfa. Pakuti uchimo, pamene unapeza chifukwa mwa lamulo, unandinyenga ine, ndi kundipha nalo. Chotero chilamulo chili choyera, ndi chilangizo chake nchoyera, ndi cholungama, ndi chabwino. Ndipo tsopano chabwino chija chinandikhalira imfa kodi? Msatero ai. Koma uchimo, kuti uoneke kuti uli uchimo, wandichitira imfa mwa chabwino chija; kuti uchimo ukakhale wochimwitsa ndithu mwa lamulo. Pakuti tidziwa kuti chilamulo chili chauzimu; koma ine ndili wathupi, wogulitsidwa kapolo wa uchimo. Pakuti chimene ndichita sindichidziwa; pakuti sindichita chimene ndifuna, koma chimene ndidana nacho, ndichita ichi. Koma ngati ndichita chimene sindichifuna, ndivomerezana nacho chilamulo kuti chili chabwino. Ndipo tsopano si ine ndichichita, koma uchimo wakukhalabe m'kati mwanga ndiwo. Pakuti ndidziwa kuti m'kati mwanga, ndiko m'thupi langa, simukhala chinthu chabwino; pakuti kufuna ndili nako, koma kuchita chabwino sindikupeza. Pakuti chabwino chimene ndichifuna, sindichichita; koma choipa chimene sindichifuna, chimenecho ndichichita. Koma ngati ndichita chimene sindichifuna, si ndinenso amene ndichichita, koma uchimo wakukhalabe m'kati mwanga ndiwo. Ndipo chotero ndipeza lamulo ili, kuti, pamene ndifuna chabwino, choipa chiliko. Pakuti monga mwa munthu wa m'kati mwanga, ine ndikondwera ndi chilamulo cha Mulungu: koma ndiona lamulo lina m'ziwalo zanga, lilikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la uchimo m'ziwalo zanga. Munthu wosauka ine; adzandilanditsa ndani m'thupi la imfa iyi? Ndiyamika Mulungu, mwa Yesu Khristu Ambuye wathu. Ndipo chotero ine ndekha ndi mtimatu nditumikira chilamulo cha Mulungu; koma ndi thupi nditumikira lamulo la uchimo. Chifukwa chake tsopano iwo akukhala mwa Khristu Yesu alibe kutsutsidwa. Pakuti chilamulo cha mzimu wa moyo mwa Khristu Yesu chandimasula ine ku lamulo la uchimo ndi la imfa. Pakuti chimene chilamulo sichinathe kuchita, popeza chinafooka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana wake wa Iye yekha m'chifanizo cha thupi la uchimo, ndi chifukwa cha uchimo, natsutsa uchimo m'thupi; kuti choikika chake cha chilamulo chikakwaniridwe mwa ife, amene sitiyendayenda monga mwa thupi, koma monga mwa mzimu. Pakuti iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo amene ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu: pakuti chisamaliro cha thupi chili imfa; koma chisamaliro cha mzimu chili moyo ndi mtendere. Chifukwa chisamaliro cha thupi chidana ndi Mulungu; pakuti sichigonja ku chilamulo cha Mulungu, pakuti sichikhoza kutero. Ndipo iwo amene ali m'thupi sangathe kukondweretsa Mulungu. Koma inu simuli m'thupi ai, koma mumzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu akhalabe mwa inu. Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Khristu, siali wake wa Khristu. Ndipo ngati Khristu akhala mwa inu, thupilo ndithu lili lakufa chifukwa cha uchimo; koma mzimu uli wamoyo chifukwa cha chilungamo. Koma ngati Mzimu wa Iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, Iye amene adaukitsa Khristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wake wakukhala mwa inu. Chifukwa chake, abale, ife tili amangawa si ake a thupi ai, kukhala ndi moyo monga mwa thupi; pakuti ngati mukhala ndi moyo monga mwa thupi, mudzafa; koma ngati ndi mzimu mufetsa zochita zake za thupi, mudzakhala ndi moyo. Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu. Pakuti inu simunalandira mzimu wa ukapolo kuchitanso mantha; koma munalandira mzimu wa umwana, umene tifuula nao, kuti, Abba! Atate! Mzimu yekha achita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tili ana a Mulungu; ndipo ngati ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ake a Mulungu, ndi olowa anzake a Khristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalandirenso ulemerero pamodzi ndi Iye. Pakuti ndiyesa kuti masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzaonetsedwa kwa ife. Pakuti chiyembekezetso cha cholengedwa chilindira vumbulutso la ana a Mulungu. Pakuti cholengedwacho chagonjetsedwa kuutsiru, chosafuna mwini, koma chifukwa cha Iye amene anachigonjetsa, ndi chiyembekezo kuti cholengedwa chomwe chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kulowa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu. Pakuti tidziwa kuti cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m'zowawa pamodzi kufikira tsopano. Ndipo si chotero chokha, koma ife tomwe, tili nazo zoundukula za Mzimu, inde ifenso tibuula m'kati mwathu, ndi kulindirira umwana wathu, ndiwo chiomboledwe cha thupi lathu. Pakuti ife tinapulumutsidwa ndi chiyembekezo; koma chiyembekezo chimene chioneka si chili chiyembekezo ai; pakuti ayembekezera ndani chimene achipenya? Koma ngati tiyembekezera chimene sitichipenya, pomwepo tichilindirira ndi chipiriro. Ndipo momwemonso Mzimu athandiza kufooka kwathu; pakuti chimene tizipempha monga chiyenera, sitidziwa; koma Mzimu mwini atipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka; ndipo Iye amene asanthula m'mitima adziwa chimene achisamalira Mzimu, chifukwa apempherera oyera mtima monga mwa chifuno cha Mulungu. Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake. Chifukwa kuti iwo amene Iye anawadziwiratu, iwowa anawalamuliratu afanizidwe ndi chifaniziro cha Mwana wake, kuti Iye akakhale mwana woyamba wa abale ambiri; ndipo amene Iye anawalamuliratu, iwo anawaitananso; ndimo iwo amene Iye anawaitana, iwowa anawayesanso olungama; ndi iwo amene Iye anawayesa olungama, iwowa anawapatsanso ulemerero. Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani? Iye amene sanatimana Mwana wake wa Iye yekha, koma anampereka chifukwa cha ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi Iye? Ndani adzaneneza osankhidwa a Mulungu? Mulungu ndiye amene awayesa olungama; ndani adzawatsutsa? Khristu Yesu ndiye amene adafera, inde makamaka, ndiye amene adauka kwa akufa, amene akhalanso pa dzanja lamanja la Mulungu, amenenso atipempherera ife. Adzatisiyanitsa ndani ndi chikondi cha Khristu? Nsautso kodi, kapena kupsinjika mtima, kapena kuzunza, kapena njala, kapena usiwa, kapena zoopsa kapena lupanga kodi? Monganso kwalembedwa, Chifukwa cha Inu tilikuphedwa dzuwa lonse; tinayesedwa monga nkhosa zakupha. Koma m'zonsezi, ife tilakatu, mwa Iye amene anatikonda. Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu. Ndinena zoona mwa Khristu, sindinama ai, chikumbu mtima changa chichita umboni pamodzi ndine mwa Mzimu Woyera, kuti ndagwidwa ndi chisoni chachikulu ndi kuphwetekwa mtima kosaleka. Pakuti ndikadafuna kuti ine ndekha nditembereredwe kundichotsa kwa Khristu chifukwa cha abale anga, ndiwo a mtundu wanga monga mwa thupi; ndiwo Aisraele; ali nao umwana, ndi ulemerero, ndi mapangano, ndi kupatsa kwa malamulo, ndi kutumikira m'Kachisi wa Mulungu, ndi malonjezo; a iwo ali makolo, ndi kwa iwo anachokera Khristu, monga mwa thupi, ndiye Mulungu wa pamwamba pa zonse wolemekezeka kunthawi zonse. Amen. Koma sikuli ngati mau a Mulungu anakhala chabe ai. Pakuti onse akuchokera kwa Israele siali Israele; kapena chifukwa ali mbeu ya Abrahamu, siali onse ana; koma anati, Mwa Isaki, mbeu yako idzaitanidwa. Ndiko kuti, ana a thupi sakhala iwo ana a Mulungu ai; koma ana a lonjezo awerengedwa mbeu yake. Pakuti mau a lonjezo ndi amenewa, Pa nyengo iyi ndidzadza, ndipo Sara adzakhala ndi mwana. Ndipo si chotero chokha, koma Rebekanso, pamene anali ndi pakati pa mmodzi, ndiye kholo lathu Isaki; pakuti anawo asanabadwe, kapena asanachite kanthu kabwino kapena koipa, kuti kutsimikiza mtima kwa Mulungu monga mwa kusankha kukhale, si chifukwa cha ntchito ai, koma chifukwa cha wakuitanayo, chotero kunanenedwa kwa uyo, Wamkulu adzakhala kapolo wa wamng'ono. Inde monga kunalembedwa, Ndinakonda Yakobo, koma ndinamuda Esau. Ndipo tsono tidzatani? Kodi chilipo chosalungama ndi Mulungu? Msatero ai. Pakuti anati ndi Mose, Ndidzachitira chifundo amene ndimchitira chifundo, ndipo ndidzakhala ndi chisoni kwa iye amene ndikhala naye chisoni. Chotero sichifuma kwa munthu amene afuna, kapena kwa iye amene athamanga, koma kwa Mulungu amene achitira chifundo. Pakuti lembo linena kwa Farao, Chifukwa cha ichi, ndinakuutsa iwe, kuti ndikaonetse mwa iwe mphamvu yanga, ndi kuti dzina langa likabukitsidwe pa dziko lonse lapansi. Chotero Iye achitira chifundo amene Iye afuna, ndipo amene Iye afuna amuumitsa mtima. Pamenepo udzanena ndine kodi, Adandaulabe bwanji? Pakuti ndani anakaniza chifuno chake? Koma munthu iwe, ndiwe yani wakubwezera Mulungu mau? Kodi chinthu chopangidwa chidzanena ndi amene anachipanga, Undipangiranji ine chotero? Kodi kapena woumba mbiya sakutha kuchita zake padothi, kuumba ndi nchinchi yomweyo chotengera chimodzi chaulemu ndi china chamanyazi? Ndipo titani ngati Mulungu, pofuna Iye kuonetsa mkwiyo wake, ndi kudziwitsa mphamvu yake, analekerera ndi chilekerero chambiri zotengera za mkwiyo zokonzekera chionongeko? Ndi kuti Iye akadziwitse ulemerero wake waukulu pa zotengera zachifundo, zimene Iye anazikonzeratu kuulemerero, ndi ife amenenso Iye anatiitana, si a mwa Ayuda okhaokha, komanso a mwa anthu amitundu? Monga atinso mwa Hoseya, Amene sanakhala anthu anga, ndidzawatcha anthu anga; ndi iye amene sanali wokondedwa, wokondedwa. Ndipo kudzali, kuti pamalo pamenepo kunanenedwa kwa iwo, Simuli anthu anga ai, pomwepo iwo adzatchedwa ana a Mulungu wamoyo. Ndipo Yesaya afuula za Israele, kuti, Ungakhale unyinji wa ana a Israele ukhala monga mchenga wa kunyanja, chotsalira ndicho chidzapulumuka. Pakuti Ambuye adzachita mau ake pa dziko lapansi, kuwatsiriza mwachidule. Ndipo monga Yesaya anati kale, Ngati Ambuye wa makamu a kumwamba sanatisiyira ife mbeu, tikadakhala monga Sodomu, ndipo tikadafanana ndi Gomora. Chifukwa chake tidzatani? Kuti amitundu amene sanatsata chilungamo, anafikira chilungamo, ndicho chilungamo cha chikhulupiriro; koma Israele, potsata lamulo la chilungamo, sanafikila lamulolo. Chifukwa chanji? Chifukwa kuti sanachitsata ndi chikhulupiriro, koma monga ngati ndi ntchito. Anakhumudwa pa mwala wokhumudwitsa; monganso kwalembedwa, kuti, Onani, ndikhazika m'Ziyoni mwala wakukhumudwa nao, ndi thanthwe lophunthwitsa; ndipo wakukhulupirira Iye sadzachita manyazi. Abale, kufunitsa kwa mtima wanga ndi pemphero langa limene ndiwapempherera kwa Mulungu, ndilo, kuti apulumuke. Pakuti ndiwachitira iwo umboni kuti ali ndi changu cha kwa Mulungu, koma si monga mwa chidziwitso. Pakuti pakusadziwa chilungamo cha Mulungu, ndipo pofuna kukhazikitsa chilungamo cha iwo okha, iwo sanagonja ku chilungamo cha Mulungu. Pakuti Khristu ali chimaliziro cha lamulo kulinga kuchilungamo kwa amene aliyense akhulupirira. Pakuti Mose walemba kuti munthu amene achita chilungamo cha m'lamulo, adzakhala nacho ndi moyo. Koma chilungamo cha chikhulupiriro chitero, Usamanena mumtima mwako, Adzakwera ndani Kumwambako? Ndiko, kutsitsako Khristu; kapena, Adzatsikira ndani ku chiphompho chakuya? Ndiko, kukweza Khristu kwa akufa, Koma chitani? Mau ali pafupi ndiwe, m'kamwa mwako, ndi mumtima mwako; ndiwo mau a chikhulupiriro, amene ife tiwalalikira: kuti ngati udzavomereza m'kamwa mwako Yesu ndiye Ambuye, ndi kukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka: pakuti ndi mtima munthu akhulupirira kutengapo chilungamo; ndi m'kamwa avomereza kutengapo chipulumutso. Pakuti lembo litere, Amene aliyense akhulupirira Iye, sadzachita manyazi. Pakuti kulibe kusiyana Myuda ndi Mgriki; pakuti Yemweyo ali Ambuye wa onse, nawachitira zolemera onse amene aitana pa Iye; pakuti, amene aliyense adzaitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka. Ndipo iwo adzaitana bwanji pa Iye amene sanamkhulupirira? Ndipo adzakhulupirira bwanji Iye amene sanamva za Iye? Ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira? Ndipo adzalalikira bwanji, ngati satumidwa? Monganso kwalembedwa, Okometsetsa ndithu ali mapazi a iwo akulalikira Uthenga Wabwino wa zinthu zabwino. Koma sanamvera Uthenga Wabwino onsewo. Pakuti Yesaya anena, Ambuye, anakhulupirira ndani zonena ife? Chomwecho chikhulupiriro chidza ndi mbiri, ndi mbiri idza mwa mau a Khristu. Koma ine nditi, Sanamva iwo kodi! Indetu, Liu lao linatulukira kudziko lonse lapansi, ndi maneno ao ku malekezero a dziko lokhalamo anthu. Koma nditi, Kodi Israele alibe kudziwa? Poyamba Mose anena, Ine ndidzachititsa inu nsanje ndi iwo amene sakhala mtundu wa anthu, ndidzakwiyitsa inu ndi mtundu wopulukira. Ndipo Yesaya alimbika mtima ndithu, nati, Ndinapezedwa ndi iwo amene sanandifuna; ndinaonekera kwa iwo amene sanandifunsa. Koma kwa Israele anena, Dzuwa lonse ndinatambalitsira manja anga kwa anthu osamvera ndi okanakana. Chifukwa chake ndinena, Mulungu anataya anthu ake kodi? Msatero ai. Pakuti inenso ndili Mwisraele, wa mbeu ya Abrahamu, wa fuko la Benjamini. Mulungu sanataya anthu ake amene Iye anawadziwiratu. Kapena simudziwa kodi chimene lembo linena za Eliya? Kuti anaumirira Mulungu poneneza Israele, kuti, Ambuye, anawapha aneneri anu, nagwetsa maguwa anu a nsembe; ndipo ine ndatsala ndekha, ndipo alikufuna moyo wanga. Koma kuyankha kwa Mulungu kudatani kwa iye? Ndinadzisiyira ndekha anthu amuna zikwi zisanu ndi ziwiri, amene sanagwadira Baala. Choteronso nthawi yatsopano chilipo chotsalira monga mwa kusankha kwa chisomo. Koma ngati kuli ndi chisomo, sikulinso ndi ntchito ai; ndipo pakapanda kutero, chisomo sichikhalanso chisomo. Ndipo chiyani tsono? Ichi chimene Israele afunafuna sanachipeza; koma osankhidwawo anachipeza, ndipo otsalawo anaumitsidwa mtima; monga kunalembedwa kuti, Mulungu anawapatsa mzimu watulo, maso kuti asapenye, ndi makutu kuti asamve, kufikira lero lino. Ndipo Davide akuti, Gome lao likhale kwa iwo, ngati msampha, ndi ngati diwa, ndi monga chokhumudwitsa, ndi chowabwezera chilango; maso ao adetsedwe, kuti asapenye, ndipo muweramitse msana wao masiku onse. Chifukwa chake ndinena, Anakhumudwa kodi kuti agwe? Msatero ai; koma ndi kulakwa kwao chipulumutso chinadza kwa anthu akunja, kudzachititsa iwo nsanje. Ndipo ngati kulakwa kwao, kwatengera dziko lapansi zolemera, ndipo kuchepa kwao kutengera anthu amitundu zolemera; koposa kotani nanga kudzaza kwao? Koma ndilankhula ndi inu anthu amitundu. Popeza ine ndili mtumwi wa anthu amitundu, ndilemekeza utumiki wanga; kuti ngati nkutheka ndikachititse nsanje anthu a mtundu wanga, ndi kupulumutsa ena a iwo. Pakuti ngati kuwataya kwao kuli kuyanjanitsa kwa dziko lapansi, nanga kulandiridwa kwao kudzatani, koma ndithu ngati moyo wakuchokera kwa akufa? Ndipo ngati zoundukula zili zopatulika, choteronso mtanda; ndipo ngati muzu uli wopatulika, choteronso nthambi. Koma ngati nthambi zina zinathyoledwa, ndipo iwe, ndiwe mtengo wa azitona wa kuthengo, unalumikizidwa mwa izo, nugawana nazo za muzu za mafuta ake a mtengowo, usadzitama iwe wekha pa nthambizo: koma ngati udzitama wekha, suli iwe amene unyamula muzu, ai, koma muzu ukunyamula iwetu. Ndipo kapena udzanena, Nthambizo zathyoledwa kuti ine ndikalumikizidwe nao. Chabwino; iwo anathyoledwa ndi kusakhulupirira kwao, ndipo iwe umaima ndi chikhulupiriro chako. Usamadzikuza mumtima, koma opatu: pakuti ngati Mulungu sanaleka nthambi za mtundu wake, inde sadzakuleka iwe. Chifukwa chake onani kukoma mtima ndi kuuma mtima kwake kwa Mulungu: kwa iwo adagwa, kuuma kwake; koma kwa iwe kukoma mtima kwake kwa Mulungu, ngati ukhala chikhalire m'kukoma mtimamo; koma ngati sutero, adzakusadza iwe. Ndipo iwonso, ngati sakhala chikhalire mu kusakhulupirira, adzawalumikizanso, pakuti Mulungu ali wamphamvu yakutha kuwalumikizanso. Pakuti ngati iwe unasadzidwa kumtengo wa azitona wa mtundu wa kuthengo, ndipo unalumikizidwa ndi mtengo wa azitona wabwino, mokaniza makhalidwe ako; koposa kotani nanga iwo, ndiwo nthambi za mtundu wake, adzalumikizidwa ndi mtengo wao womwewo wa azitona? Pakuti sindifuna, abale, kuti mukhale osadziwa chinsinsi ichi, kuti mungadziyese anzeru mwa inu nokha, kuti kuuma mtima kunadza pang'ono pa Israele, kufikira kudzaza kwa anthu amitundu kunalowa; ndipo chotero Israele yense adzapulumuka; monganso kunalembedwa, kuti, Adzatuluka ku Ziyoni Mpulumutsi; Iye adzachotsa zamwano kwa Yakobo: Ndipo ichi ndi chipangano changa ndi iwo, pamene ndidzachotsa machimo ao. Kunena za Uthenga Wabwino, iwo ali ngati adani, chifukwa cha inu; koma kunena za chisankhidwe, ali okondedwa, chifukwa cha makolo. Pakuti mphatso zake ndi kuitana kwake kwa Mulungu sizilapika. Pakuti monga inunso kale simunamvera Mulungu, koma tsopano mwalandira chifundo mwa kusamvera kwao, choteronso iwo sanamvera tsopano, kuti iwonso akalandire chifundo, chifukwa cha chifundo cha kwa inu. Pakuti Mulungu anatsekera pamodzi onse m'kusamvera, kuti akachitire onse chifundo. Ha! Kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake nzosalondoleka! Pakuti anadziwitsa ndani mtima wake wa Ambuye? Kapena anakhala mphungu wake ndani? Ndipo anayamba ndani kumpatsa Iye, ndipo adzambwezeranso? Chifukwa zinthu zonse zichokera kwa Iye, zichitika mwa Iye, ndi kufikira kwa Iye. Kwa Iyeyo ukhale ulemerero kunthawi zonse. Amen. Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera. Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro. Pakuti ndi chisomo chapatsidwa kwa ine, ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga Mulungu anagawira kwa munthu aliyense muyeso wa chikhulupiriro. Pakuti monga m'thupi limodzi tili nazo ziwalo zambiri, ndipo ziwalo zonsezo sizili nayo ntchito imodzimodzi; chomwecho ife, ndife ambiri, tili thupi limodzi mwa Khristu, ndi ziwalo zinzake, wina ndi wina. Ndipo pokhala ife ndi mphatso zosiyana, monga mwa chisomo chipatsidwa kwa ife, kapena mphatso yakunenera, tinenere monga mwa muyeso wa chikhulupiriro; kapena yakutumikira, tidzipereke ku utumiki uwu; kapena iye wakuphunzitsa, kukuphunzitsako; kapena iye wakudandaulira, kukudandaulirako; wakugawira achite ndi mtima woona; iye wakuweruza, aweruze ndi changu; iye wakuchita chifundo, achite ndi kukondwa mtima. Chikondano chikhale chopanda chinyengo. Dana nacho choipa; gwirizana nacho chabwino. M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu; musakhale aulesi m'machitidwe anu; khalani achangu mumzimu, tumikirani Ambuye; kondwerani m'chiyembekezo, pirirani m'masautso; limbikani chilimbikire m'kupemphera. Patsani zosowa oyera mtima; cherezani aulendo. Dalitsani iwo akuzunza inu; dalitsani, musawatemberere. Kondwani nao iwo akukondwera; lirani nao akulira. Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake. Musasamalire zinthu zazikulu, koma phatikanani nao odzichepetsa. Musadziyesere anzeru mwa inu nokha. Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse. Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse. Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye. Koma ngati mdani wako akumva njala, umdyetse, ngati akumva ludzu, ummwetse; pakuti pakutero udzaunjika makala a moto pamutu pake. Musagonje kwa choipa, koma ndi chabwino gonjetsani choipa. Anthu onse amvere maulamuliro a akulu; pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu; ndipo iwo amene alipo aikidwa ndi Mulungu. Kotero kuti iye amene atsutsana nao ulamuliro, akaniza choikika ndi Mulungu; ndipo iwo akukaniza, adzadzitengera kulanga. Pakuti mafumu sakhala oopsa ntchito zabwino koma zoipa. Ndipo ufuna kodi kusaopa ulamuliro? Chita chabwino, ndipo udzalandira kutama m'menemo: pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu, kuchitira iwe zabwino. Koma ngati uchita choipa, opatu, pakuti iye sagwira lupanga kwachabe; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu wakukwiyira ndi kubwezera chilango wochita zoipa. Chifukwa chake, kuyenera kuti mukhale omvera, si chifukwa cha mkwiyo wokha, komanso chifukwa cha chikumbu mtima. Pakuti chifukwa cha ichi mupatsanso msonkho; pakuti iwo ndiwo atumiki a Mulungu akulabadirabe chinthu chimenechi. Perekani kwa anthu onse mangawa ao; msonkho kwa eni ake a msonkho; kulipira kwa eni ake a kulipidwa; kuopa kwa eni ake a kuwaopa; ulemu kwa eni ake a ulemu. Musakhale ndi mangawa kwa munthu aliyense, koma kukondana ndiko; pakuti iye amene akondana ndi mnzake wakwanitsa lamulo. Pakuti ili, Usachite chigololo, Usaphe, Usabe, Usasirire, ndipo lingakhale lamulo lina lililonse, limangika pamodzi m'mau amenewa, kuti, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe wekha. Chikondano sichichitira mnzake choipa; chotero chikondanocho chili chokwanitsa lamulo. Ndipo chitani ichi, podziwa inu nyengo, kuti tsopano ndiyo nthawi yabwino yakuuka kutulo; pakuti tsopano chipulumutso chathu chili pafupi koposa pamene tinayamba kukhulupirira. Usiku wapita, ndi mbandakucha wayandikira; chifukwa chake tivule ntchito za mdima, ndipo tivale zida za kuunika. Tiyendeyende koyenera, monga usana; si m'madyerero ndi kuledzera ai, si m'chigololo ndi chonyansa ai, si mu ndeu ndi nkhwidzi ai. Koma valani inu Ambuye Yesu Khristu, ndipo musaganizire za thupi kuchita zofuna zake. Ndipo iye amene ali wofooka m'chikhulupiriro, mumlandire, koma si kuchita naye makani otsutsana ai. Munthu mmodzi akhulupirira kuti adye zinthu zonse, koma wina wofooka angodya zitsamba. Wakudyayo asapeputse wosadyayo; ndipo wosadyayo asaweruze wakudyayo; pakuti Mulungu wamlandira. Ndani iwe wakuweruza mnyamata wa mwini wake? Iye aimirira kapena kugwa kwa mbuye wake wa mwini yekha. Ndipo adzaimiritsidwa; pakuti Ambuye ali wamphamvu kumuimiritsa. Munthu wina aganizira kuti tsiku lina liposa linzake; wina aganizira kuti masiku onse alingana. Munthu aliyense akhazikike konse mumtima mwake. Iye wakusamalira tsiku, alisamalira kwa Ambuye: ndipo iye wakudya, adya mwa Ambuye, pakuti ayamika Mulungu; ndipo iye wosadya, mwa Ambuye sakudya, nayamikanso Mulungu. Pakuti palibe mmodzi wa ife adzikhalira ndi moyo yekha, ndipo palibe mmodzi adzifera yekha. Pakuti tingakhale tili ndi moyo, tikhalira Ambuye moyo; kapena tikafa, tifera Ambuye; chifukwa chake tingakhale tili ndi moyo, kapena tikafa, tikhala ake a Ambuye. Pakuti, chifukwa cha ichi Khristu adafera, nakhalanso ndi moyo, kuti Iye akakhale Ambuye wa akufa ndi wa amoyo. Koma iwe uweruziranji mbale wako? Kapena iwenso upeputsiranji mbale wako? Pakuti ife tonse tidzaimirira kumpando wakuweruza wa Mulungu. Pakuti kwalembedwa, Pali moyo wanga, ati Ambuye, mabondo onse adzagwadira Ine, ndipo malilime onse adzavomereza Mulungu. Chotero munthu aliyense wa ife adzadziwerengera mlandu wake kwa Mulungu. Chifukwa chake tisaweruzanenso wina mnzake; koma weruzani ichi makamaka, kuti munthu asaike chokhumudwitsa pa njira ya mbale wake, kapena chomphunthwitsa. Ndidziwa, ndipo ndakhazikika mtima mwa Ambuye Yesu, kuti palibe chinthu chonyansa pa chokha; koma kwa ameneyo achiyesa chonyansa, kwa iye chikhala chonyansa. Koma ngati iwe wachititsa mbale wako chisoni ndi chakudya, pamenepo ulibe kuyendayendanso ndi chikondano. Usamuononga ndi chakudya chako, iye amene Khristu adamfera. Chifukwa chake musalole chabwino chanu achisinjirire. Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala chakudya ndi chakumwa, koma chilungamo, ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera. Pakuti iye amene atumikira Khristu mu izi akondweretsa Mulungu, navomerezeka ndi anthu. Chifukwa chake tilondole zinthu za mtendere, ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mnzake. Usapasule ntchito ya Mulungu chifukwa cha chakudya. Zinthu zonse zili zoyera; koma kuli koipa kwa munthu amene akudya ndi kukhumudwa. Kuli kwabwino kusadya nyama, kapena kusamwa vinyo, kapena kusachita chinthu chilichonse chakukhumudwitsa mbale wako. Chikhulupiriro chimene uli nacho, ukhale nacho kwa iwe wekha pamaso pa Mulungu. Wodala ndiye amene sadziweruza mwini yekha m'zinthu zomwe iye wazivomereza. Koma iye amene akayikakayika pakudya, atsutsika, chifukwa akudya wopanda chikhulupiriro; ndipo chinthu chilichonse chosatuluka m'chikhulupiriro, ndicho uchimo. Ndipo ife amene tili olimba tiyenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha. Yense wa ife akondweretse mnzake, kumchitira zabwino, zakumlimbikitsa. Pakuti Khristunso sanadzikondweretsa yekha; koma monga kwalembedwa, Minyozo ya iwo amene anakunyoza iwe inagwa pa Ine. Pakuti zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo. Ndipo Mulungu wa chipiriro ndi wa chitonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake, monga mwa Khristu Yesu; kuti nonse pamodzi, m'kamwa mmodzi, mukalemekeze Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu. Chifukwa chake mulandirane wina ndi mnzake, monganso Khristu anakulandirani inu, kukachitira Mulungu ulemerero. Ndipo ndinena kuti Khristu anakhala mtumiki wa mdulidwe, chifukwa cha choonadi cha Mulungu, kuti alimbikitse malonjezo opatsidwa kwa makolo, ndi kuti anthu a mitundu ina akalemekeze Mulungu, chifukwa cha chifundo; monga kwalembedwa, Chifukwa cha ichi ndidzakuvomerezani Inu pakati pa anthu amitundu, ndidzaimbira dzina lanu. Ndiponso anena, Kondwani, amitundu inu, pamodzi ndi anthu ake. Ndiponso, Tamandani Ambuye, inu a mitundu yonse; ndipo anthu onse amtamande. Ndiponso, Yesaya ati, Padzali muzu wa Yese, ndi Iye amene aukira kuchita ufumu pa anthu amitundu; Iyeyo anthu amitundu adzamuyembekezera. Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera. Koma ine ndekhanso, abale anga, nditsimikiza mtima za inu, kuti inu nokhanso muli odzala ndi ubwino, odzazidwa ndi kudziwitsa konse, ndi kukhoza kudandaulirana wina ndi mnzake. Koma mwina ndaposa kukulemberani molimba mtima monga kukukumbutsaninso, chifukwa cha chisomo chapatsidwa kwa ine ndi Mulungu, kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kupereka kwake kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera. Chifukwa chake ndili nacho chodzitamandira cha m'Khristu Yesu ndi zinthu za kwa Mulungu. Pakuti sindingathe kulimba mtima kulankhula zinthu zimene Khristu sanazichita mwa ine zakumveretsa anthu amitundu, ndi mau ndi ntchito, mu mphamvu ya zizindikiro ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu Woyera; kotero kuti ine kuyambira ku Yerusalemu ndi kuzungulirako kufikira ku Iliriko, ndinakwanitsa Uthenga Wabwino wa Khristu; ndipo chotero ndinachiyesa chinthu chaulemu kulalikira Uthenga Wabwino, pa malopo Khristu asanatchulidwe kale, kuti ndisamange nyumba pa maziko a munthu wina. Koma monga kwalembedwa, Iwo amene uthenga wake sunawafikire, adzaona, ndipo iwo amene sanamve, adzadziwitsa. Chifukwa chakenso ndinaletsedwa kawirikawiri kudza kwa inu; koma tsopano, pamene ndilibe malo m'maiko akuno, ndipo pokhala ndi kulakalaka zaka zambiri kudza kwa inu, ndidzatero, pamene paliponse ndidzapita ku Spaniya. Pakuti ndiyembekeza kuonana ndi inu pa ulendo wanga, ndi kuperekezedwa ndi inu panjira panga kumeneko, ngati nditayamba kukhuta pang'ono ndi kukhala ndi inu. Koma tsopano ndipita ku Yerusalemu, ndilikutumikira oyera mtima. Pakuti kunakondweretsa a ku Masedoniya ndi Akaya kuchereza osauka a kwa oyera mtima a ku Yerusalemu. Pakuti kunakondweretsa iwo; ndiponso iwo ali amangawa ao. Pakuti ngati amitundu anagawana zinthu zao zauzimu, alinso amangawa akutumikira iwo ndi zinthu zathupi. Koma pamene ndikatsiriza ichi, ndi kuwasindikizira iwo chipatso ichi, ndidzapyola kwanu kupita ku Spaniya. Ndipo ndidziwa kuti pamene ndikadza kwanu, ndidzafika m'kudzaza kwake kwa chidalitso cha Khristu. Ndipo ndikudandaulirani, abale, ndi Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi chikondi cha Mzimu, kuti mudzalimbike pamodzi ndi ine m'mapemphero anu kwa Mulungu chifukwa cha ine; kuti ndikapulumutsidwe kwa osamvera aja a ku Yudeya; ndi kuti utumiki wanga wa ku Yerusalemu ukhale wolandiridwa bwino ndi oyera mtima; kuti ndi chimwemwe ndikadze kwa inu mwa chifuno cha Mulungu, ndi kupumula pamodzi ndi inu. Ndipo Mulungu wa mtendere akhale ndi inu nonse. Amen. Ndipereka kwa inu Febe, mlongo wathu, ndiye mtumiki wamkazi wa Mpingo wa Ambuye wa ku Kenkrea; kuti mumlandire iye mwa Ambuye, monga kuyenera oyera mtima, ndi kuti mumthandize m'zinthu zilizonse adzazifuna kwa inu; pakuti iye yekha anali wosungira ambiri, ndi ine ndemwe. Mupereke moni kwa Prisika ndi Akwila, antchito anzanga mwa Khristu Yesu, amene anapereka khosi lao chifukwa cha moyo wanga; amene ndiwayamika, si ine ndekha, komanso Mipingo yonse ya Ambuye ya kwa anthu amitundu; ndipo mupereke moni kwa Mpingo wa Ambuye wa m'nyumba mwao. Moni kwa Epeneto wokondedwa wanga, ndiye chipatso choundukula cha Asiya cha kwa Khristu. Moni kwa Maria amene anadzilemetsa ndi ntchito zambiri zothandiza inu. Moni kwa Androniko ndi Yunia, anansi anga, ndi andende anzanga, amene ali omveka mwa atumwi, amenenso ananditsogolera ine mwa Khristu. Moni kwa Ampiliato wokondedwa wanga mwa Ambuye. Moni kwa Urbano wantchito mnzathu mwa Khristu, ndi Stakisi wokondedwa wanga. Moni kwa Apelesi, wovomerezedwayo mwa Khristu. Moni iwo a kwa Aristobulo. Moni kwa Herodiono, mbale wanga. Moni iwo a kwa Narkiso, amene ali mwa Ambuye. Moni kwa Trifena, ndi Trifosa amene agwiritsa ntchito mwa Ambuye. Moni kwa Perisi, wokondedwayo amene anagwiritsa ntchito zambiri mwa Ambuye. Moni kwa Rufu, wosankhidwayo mwa Ambuye, ndi amai wake ndi wanga. Moni kwa Asinkrito, Filegoni, Heremesi, Patrobasi, Herimasi ndi abale amene ali nao. Moni Filologo ndi Juliya, Nereo ndi mlongo wake, ndi Olimpasi, ndi oyera mtima onse ali pamodzi nao. Mupatsane moni wina ndi mnzake ndi kupsompsona kupatulika. Mipingo yonse ya Khristu ikupatsani moni. Ndipo ndikudandaulirani, abale, yang'anirani iwo akuchita zopatutsana ndi zophunthwitsa, kosalingana ndi chiphunzitsocho munachiphunzira inu; ndipo potolokani pa iwo. Pakuti otere satumikira Ambuye wathu Khristu, koma mimba yao; ndipo ndi mau osalaza ndi osyasyalika asocheretsa mitima ya osalakwa. Pakuti kumvera kwanu kunabuka kwa anthu onse. Chifukwa chake ndikondwera ndi inu; koma ndifuna kuti mukakhale anzeru pa zabwino, koma ozungulidwa pa zoipa. Ndipo Mulungu wa mtendere adzaphwanya Satana pansi pa mapazi anu tsopano lino. Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse. Timoteo wantchito mnzanga akupatsani moni; ndi Lusio ndi Yasoni ndi Sosipatere, abale anga. Ine Tersio, ndilikulemba kalata ameneyu, ndikupereka moni mwa Ambuye. Gayo, mwini nyumba wolandira ine, ndi Mpingo wonse wa Ambuye, akupereka moni. Erasto, ndiye woyang'anira mudzi, akupereka moni, ndiponso Kwarto mbaleyo. *** Ndipo kwa Iye amene ali wamphamvu yakukhazikitsa inu monga mwa Uthenga wanga Wabwino, ndi kulalikira kwa Yesu Khristu, monga mwa vumbulutso la chinsinsi chimene chinabisika mwa nthawi zonse zosayamba, koma chaonetsedwa tsopano, ndi kudziwidwa kwa anthu a mitundu yonse mwa malembo a aneneriwo, monga mwa lamulo la Mulungu wosatha, kuti amvere chikhulupiriro; kwa Mulungu wanzeru yekhayo, mwa Yesu Khristu, kwa yemweyo ukhale ulemerero kunthawi zonse. Amen. Paulo, woitanidwa akhale mtumwi wa Khristu Yesu mwa chifuniro cha Mulungu, ndi Sostene mbaleyo, kwa Mpingo wa Mulungu wakukhala m'Korinto, ndiwo oyeretsedwa mwa Khristu Yesu, oitanidwa akhale oyera mtima, pamodzi ndi onse akuitana pa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, m'malo monse, ndiye wao, ndi wathu: Chisomo kwa inu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu. Ndiyamika Mulungu wanga nthawi yonse kaamba ka inu, chifukwa cha chisomo cha Mulungu chinapatsidwa kwa inu mwa Khristu Yesu; kuti m'zonse munalemezedwa mwa Iye, m'mau onse, ndi chidziwitso chonse; monga umboni wa Khristu unakhazikika mwa inu; kotero kuti sichikusowani inu chaufulu chilichonse; pakulindira inu vumbulutso la Ambuye wathu Yesu Khristu; amenenso adzakukhazikitsani inu kufikira chimaliziro, kuti mukhale opanda chifukwa m'tsiku la Ambuye wathu Yesu Khristu. Mulungu ali wokhulupirika amene munaitanidwa mwa Iye, ku chiyanjano cha Mwana wake Yesu Khristu, Ambuye wathu. Koma ndikudandaulirani inu, abale, mwa dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti munene chimodzimodzi inu nonse, ndi kuti pasakhale malekano pakati pa inu; koma mumangike mu mtima womwewo ndi m'chiweruziro chomwecho. Pakuti zinamveka kwa ine za inu, abale anga, ndi iwo a kwa Koloe, kuti pali makani pakati pa inu. Koma ichi ndinena, kuti yense wa inu anena, Ine ndine wa Paulo; koma ine wa Apolo; koma ine wa Kefa; koma ine wa Khristu. Kodi Khristu wagawika? Kodi Paulo anapachikidwa chifukwa cha inu? Kapena kodi munabatizidwa m'dzina la Paulo? Ndiyamika Mulungu kuti sindinabatiza mmodzi yense wa inu, koma Krispo ndi Gayo; kuti anganene mmodzi kuti mwabatizidwa m'dzina langa. Koma ndinabatizanso a pa banja la Stefanasi; za ena, sindidziwa ngati ndinabatiza wina yense. Pakuti Khristu sanandituma ine kubatiza, koma kulalikira Uthenga Wabwino, si mu nzeru ya mau, kuti mtanda wa Khristu ungayesedwe wopanda pake. Pakuti mau a mtanda ali ndithu chinthu chopusa kwa iwo akutayika, koma kwa ife amene tilikupulumutsidwa ali mphamvu ya Mulungu. Pakuti kulembedwa, Ndidzaononga nzeru za anzeru, ndi kuchenjera kwa ochenjera ndidzakutha. Ali kuti wanzeru? Mlembi ali kuti? Ali kuti wotsutsana wa nthawi ya pansi pano? Kodi Mulungu sanaipusitsa nzeru ya dziko lapansi? Pakuti popeza m'nzeru ya Mulungu dziko lapansi, mwa nzeru yake, silinadziwa Mulungu, chidamkonda Mulungu kupulumutsa okhulupirirawo mwa chopusa cha kulalikira. Ndipo popeza Ayuda afunsa zizindikiro, ndi Agriki atsata nzeru: koma ife tilalikira Khristu wopachikidwa, kwa Ayudatu chokhumudwitsa, ndi kwa amitundu chinthu chopusa; koma kwa iwo oitanidwa, ndiwo Ayuda ndi Agriki, Khristu mphamvu ya Mulungu, ndi nzeru ya Mulungu. Chifukwa kuti chipusa cha Mulungu chiposa anthu ndi nzeru zao; ndipo chofooka cha Mulungu chiposa anthu ndi mphamvu yao. Pakuti penyani maitanidwe anu, abale, kuti saitanidwa ambiri anzeru, monga mwa thupi; ambiri amphamvu, mfulu zambiri, iai; koma Mulungu anasankhula zopusa za dziko lapansi, kuti akachititse manyazi anzeru; ndipo zofooka za dziko lapansi Mulungu anazisankhula, kuti akachititse manyazi zamphamvu; ndipo zopanda pake za dziko lapansi, ndi zonyozeka, anazisankhula Mulungu, ndi zinthu zoti kulibe; kuti akathere zinthu zoti ziliko; kuti thupi lililonse lisadzitamande pamaso pa Mulungu. Koma kwa Iye muli inu mwa Khristu Yesu, amene anayesedwa kwa ife nzeru ya kwa Mulungu, ndi chilungamo ndi chiyeretso ndi chiombolo; kuti monga mwalembedwa, Iye amene adzitamanda, adzitamande mwa Ambuye. Ndipo ine, abale, m'mene ndinadza kwa inu, sindinadza ndi kuposa kwa mau, kapena kwa nzeru, polalikira kwa inu chinsinsi cha Mulungu. Pakuti ndinatsimikiza mtima kuti ndisadziwe kanthu mwa inu, koma Yesu Khristu, ndi Iye wopachikidwa. Ndipo ine ndinakhala nanu mofooka ndi m'mantha, ndi monthunthumira mwambiri. Ndipo mau anga ndi kulalikira kwanga sanakhala ndi mau okopa a nzeru, koma m'chionetso cha Mzimu ndi cha mphamvu; kuti chikhulupiriro chanu chisakhale m'nzeru ya anthu, koma mu mphamvu ya Mulungu. Koma tilankhula nzeru mwa angwiro; koma si nzeru ya nthawi yino ya pansi pano, kapena ya akulu a nthawi yino ya pansi pano, amene alinkuthedwa; koma tilankhula nzeru ya Mulungu m'chinsinsi, yobisikayo, imene Mulungu anaikiratu, pasanakhale nyengo za pansi pano, ku ulemerero wathu, imene saidziwa mmodzi wa akulu a nthawi ya pansi pano: pakuti akadadziwa sakadapachika Mbuye wa ulemerero; koma monga kulembedwa, Zimene diso silinaziona, ndi khutu silinazimva, nisizinalowa mu mtima wa munthu, zimene zilizonse Mulungu anakonzereratu iwo akumkonda Iye. Koma kwa ife Mulungu anationetsera izi mwa Mzimu; pakuti Mzimu asanthula zonse, zakuya za Mulungu zomwe. Pakuti ndani wa anthu adziwa za munthu, koma mzimu wa munthuyu uli mwa iye? Momwemonso za Mulungu palibe wina azidziwa, koma Mzimu wa Mulungu. Koma sitinalandira ife mzimu wa dziko lapansi, koma Mzimu wa kwa Mulungu, kuti tikadziwe zimene zipatsidwa kwa ife ndi Mulungu kwaufulu. Zimenenso tilankhula, si ndi mau ophunzitsidwa ndi nzeru za munthu, koma ophunzitsidwa ndi Mzimu; ndi kulinganiza zamzimu ndi zamzimu. Koma munthu wa chibadwidwe cha umunthu salandira za Mzimu wa Mulungu: pakuti aziyesa zopusa; ndipo sakhoza kuzizindikira, chifukwa ziyesedwa mwauzimu. Koma iye amene ali wauzimu ayesa zonse, koma iye yekha sayesedwa ndi mmodzi yense. Pakuti wadziwa ndani mtima wa Ambuye, kuti akamlangize Iye? Koma ife tili nao mtima wa Khristu. Ndipo ine, abale, sindinakhoza kulankhula ndi inu monga ndi auzimu, koma monga athupi, monga makanda mwa Khristu. Ndinadyetsa inu mkaka, si chakudya cholimba ai; pakuti simunachikhoza; ngakhale tsopano lino simuchikhoza; pakuti mulinso athupi; pakuti, pokhala pali nkhwidzi ndi ndeu pakati pa inu simuli athupi kodi, ndi kuyendayenda monga mwa munthu? Pakuti pamene wina anena, Ine ndine wa Paulo; koma mnzake, Ndine wa Apolo; simuli anthu kodi? Ndipo Apolo nchiyani, ndi Paulo nchiyani? Atumiki amene munakhulupirira mwa iwo, yense monga Ambuye anampatsa. Ndinaoka ine, anathirira Apolo; koma Mulungu anakulitsa. Chotero sali kanthu kapena wookayo, kapena wothirirayo; koma Mulungu amene akulitsa. Koma wookayo ndi wothirirayo ali amodzi; koma yense adzalandira mphotho yake ya iye yekha, monga mwa kuchititsa kwake kwa iye yekha. Pakuti ife ndife antchito anzake a Mulungu; chilimo cha Mulungu, chimango cha Mulungu ndi inu. Monga mwa chisomo cha Mulungu chidapatsidwa kwa ine, ngati mwini mamangidwe waluso, ndinaika maziko, koma wina amangapo. Koma yense ayang'anire umo amangira pamenepo. Pakuti palibe munthu akhoza kuika maziko ena, koma amene aikidwako, ndiwo Yesu Khristu. Koma ngati wina amanga pa mazikowo, golide, siliva, miyala ya mtengo wake, mtengo, udzu, dziputu, ntchito ya yense idzaonetsedwa; pakuti tsikulo lidzaisonyeza, chifukwa kuti yavumbululuka m'moto; ndipo moto wokha udzayesera ntchito ya yense ikhala yotani. Ngati ntchito ya munthu aliyense ikhala imene anaimangako, adzalandira mphotho. Ngati ntchito ya wina itenthedwa, zidzaonongeka zake; koma iye yekha adzapulumutsidwa; koma monga momwe mwa moto. Kodi simudziwa kuti muli Kachisi wa Mulungu, ndi kuti Mzimu wa Mulungu agonera mwa inu? Ngati wina aononga Kachisi wa Mulungu, ameneyo Mulungu adzamuononga; pakuti Kachisi wa Mulungu ali wopatulika, ameneyo ndi inu. Munthu asadzinyenge yekha; ngati wina ayesa kuti ali wanzeru mwa inu m'nthawi yino ya pansi pano, akhale wopusa, kuti akakhale wanzeru. Pakuti nzeru ya dziko lino lapansi ili yopusa kwa Mulungu. Pakuti kwalembedwa, Iye agwira anzeru m'chenjerero lao; ndiponso Ambuye azindikira zolingirira za anzeru, kuti zili zopanda pake. Chifukwa chake palibe mmodzi adzitamande mwa anthu. Pakuti zinthu zonse nzanu; ngati Paulo, kapena Apolo, kapena Kefa, kapena dziko lapansi, kapena moyo, kapena imfa, kapena za makono ano, kapena zilinkudza; zonse ndi zanu; koma inu ndinu a Khristu; ndi Khristu ndiye wa Mulungu. Chotero munthu atiyese ife, monga atumiki a Khristu, ndi adindo a zinsinsi za Mulungu. Komatu pano pafunika za adindo, kuti munthu akhale wokhulupirika. Koma kwa ine kuli kanthu kakang'ono ndithu kuti ndiweruzidwe ndi inu, kapena pa bwalo la munthu; koma sindiweruza ngakhale ndekha. Pakuti sindidziwa kanthu kakundipalamulitsa; koma m'menemo sindiyesedwa wolungama; koma wondiweruza ine ndiye Ambuye. Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu. Koma izi, abale, ndadziphiphiritsira ndekha ndi Apolo, chifukwa cha inu, kuti mwa ife mukaphunzire kusapitirira zimene zilembedwa; kuti pasakhale mmodzi wodzitukumulira mnzake ndi kukana wina. Pakuti akusiyanitsa iwe ndani? Ndipo uli nacho chiyani chosati wachilandira? Koma ngati wachilandira udzitamanda bwanji, monga ngati sunachilandira? Mwadzala kale, mwalemerera kale, mwachita ufumu opanda ife; ndipo mwenzi muchitadi ufumu, kuti ifenso tikachite ufumu pamodzi ndi inu. Pakuti ndiyesa, kuti Mulungu anaoneketsa ife atumwi otsiriza, monga titi tife; pakuti takhala ife choonetsedwa kudziko lapansi, ndi kwa angelo, ndi kwa anthu. Tili opusa ife chifukwa cha Khristu, koma muli ochenjera inu mwa Khristu; tili ife ofooka, koma inu amphamvu; inu ndinu olemekezeka, koma ife ndife onyozeka. Kufikira nthawi yomwe yino timva njala, timva ludzu, tili amaliseche, tikhomedwa, tilibe pokhazikika; ndipo tigwiritsa ntchito, ndi kuchita ndi manja athu a ife tokha; polalatidwa tidalitsa; pozunzidwa, tipirira; ponamizidwa, tipempha; takhala monga zonyansa za dziko lapansi, litsiro la zinthu zonse, kufikira tsopano. Sindilembera izi kukuchititsani manyazi, koma kuchenjeza inu monga ana anga okondedwa. Pakuti mungakhale muli nao aphunzitsi zikwi khumi mwa Khristu, mulibe atate ambiri; pakuti mwa Khristu Yesu ine ndinabala inu mwa Uthenga Wabwino. Chifukwa chake ndikupemphani, khalani akutsanza ine. Chifukwa cha ichi ndatuma kwa inu Timoteo, ndiye mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye, amene adzakumbutsa inu njira zanga za mwa Khristu, monga ndiphunzitsa ponsepo m'Mipingo yonse. Koma ena adzitukumula, monga ngati sindinalinkudza kwa inu. Koma ndidzafika kwa inu msanga, akandilola Ambuye; ndipo ndidzazindikira si mau a iwo odzitukumula, koma mphamvuyi. Pakuti ufumu wa Mulungu suli m'mau, koma mumphamvu. Mufuna chiyani? Kodi ndifike kwa inu ndi ndodo, kapena mwachikondi, ndi mzimu wakufatsa? Kwamveka ndithu kuti kuli chigololo pakati pa inu, ndipo chigololo chotere chonga sichimveka mwa amitundu, kuti wina ali naye mkazi wa atate wake. Ndipo mukhala odzitukumula, kosati makamaka mwachita chisoni, kuti achotsedwe pakati pa inu iye amene anachita ntchito iyi. Pakuti inedi, thupi langa kulibe, koma mzimu wanga ulipo, ndaweruza kale, monga ngati ndilipo, m'dzina la Ambuye wathu Yesu, posonkhana pamodzi inu ndi mzimu wanga, ndi mphamvu ya Ambuye wathu Yesu, kumpereka iye wochita chotere kwa Satana, kuti lionongeke thupi, kuti mzimu upulumutsidwe m'tsiku la Ambuye Yesu. Kudzitamanda kwanu sikuli bwino. Kodi simudziwa kuti chotupitsa pang'ono chitupitsa mtanda wonse? Tsukani chotupitsa chakale, kuti mukakhale mtanda watsopano, monga muli osatupa. Pakutinso Paska wathu waphedwa, ndiye Khristu; chifukwa chake tichita phwando, si ndi chotupitsa chakale, kapena ndi chotupitsa cha dumbo, ndi kuipa mtima, koma ndi mkate wosatupa wa kuona mtima, ndi choonadi. Ndinalembera inu m'kalata uja, kuti musayanjane ndi achigololo; si konsekonse ndi achigololo a dziko lino lapansi, kapena ndi osirira, ndi okwatula, kapena ndi opembedza mafano; pakuti nkutero mukatuluke m'dziko lapansi; koma tsopano ndalembera inu kuti musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wachigololo, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, kungakhale kukadya naye wotere, iai. Pakuti nditani nao akunja kukaweruza iwo? Kodi amene ali m'katimo simuwaweruza ndi inu, koma akunja awaweruza Mulungu? Chotsani woipayo pakati pa inu nokha. Kodi akhoza wina wa inu, pamene ali nao mlandu pa mnzake, kupita kukaweruzidwa kwa osalungama, osati kwa oyera mtima? Kapena kodi simudziwa kuti oyera mtima adzaweruza dziko lapansi? Ndipo ngati dziko lapansi liweruzidwa ndi inu, muli osayenera kodi kuweruza timilandu tochepachepa? Kodi simudziwa kuti tidzaweruza angelo? Koposa kotani nanga zinthu za moyo uno? Chifukwa chake, ngati muli nayo milandu ya zinthu za moyo uno, kodi muweruzitsa iwo amene ayesedwa achabe mu Mpingo? Ndinena ichi kukuchititsani inu manyazi. Kodi nkutero kuti mwa inu palibe mmodzi wanzeru, amene adzakhoza kuweruza pa abale, koma mbale anena mlandu ndi mbale, ndikotu kwa osakhulupirira? Koma pamenepo pali chosowa konsekonse mwa inu, kuti muli nayo milandu wina ndi mnzake. Chifukwa ninji simusankhula kulola kuipsidwa? Simusankhula chifukwa ninji kulola kunyengedwa? Koma muipsa, nimunyenga, ndipo mutero nao abale anu. Kapena simudziwa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna, kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzalowa Ufumu wa Mulungu. Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m'dzina la Ambuye Yesu Khristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu. Zinthu zonse ziloledwa kwa ine; koma si zonse zipindula. Zinthu zonse ziloledwa kwa ine, koma sindidzalamulidwa nacho chimodzi. Zakudya ndizo za mimba, ndi mimba ndiyo ya zakudya; koma Mulungu adzathera iyi ndi izi. Koma thupi silili la chigololo, koma la Ambuye, ndi Ambuye wa thupi; koma Mulungu anaukitsa Ambuye, ndiponso adzaukitsa ife mwa mphamvu yake. Kodi simudziwa kuti matupi anu ali ziwalo za Khristu? Chifukwa chake ndidzatenga ziwalo za Khristu kodi, ndi kuziyesa ziwalo za mkazi wachiwerewere? Msatero iai. Kapena simudziwa kuti iye wophatikidwa ndi mkazi wachiwerewere ali thupi limodzi? Pakuti awiriwo, ati, adzakhala thupi limodzi. Koma iye wophatikidwa ndi Ambuye ali mzimu umodzi. Thawani dama. Tchimo lililonse munthu akalichita lili kunja kwa thupi; koma wachiwerewere achimwira thupi lake la iye yekha. Kapena simudziwa kuti thupi lanu lili Kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha. Pakuti munagulidwa ndi mtengo wake wapatali; chifukwa chake lemekezani Mulungu m'thupi lanu. Koma za izi munalembazi; kuli bwino kwa munthu kusakhudza mkazi. Koma chifukwa cha madama munthu yense akhale naye mkazi wa iye yekha, ndi mkazi yense akhale naye mwamuna wa iye yekha. Mwamunayo apereke kwa mkazi mangawa ake; koma modzimodzinso mkazi kwa mwamuna. Mkazi alibe ulamuliro wa pa thupi lake la iye yekha, koma mwamuna ndiye; koma momwemonso mwamuna alibe ulamuliro wa pa thupi la iye yekha, koma mkazi ndiye. Musakanizana, koma ndi kuvomerezana kwanu ndiko, kwa nthawi, kuti mukadzipereke kwa kupemphera, nimukakhalenso pamodzi, kuti Satana angakuyeseni, chifukwa cha kusadziletsa kwanu. Koma ichi ndinena monga mwa kulola, si monga mwa kulamulira. Koma mwenzi anthu onse akadakhala monga momwe ndili ine ndekha. Koma munthu yense ali nayo mphatso yake ya iye yekha kwa Mulungu, wina chakuti, wina chakuti. Koma ndinena kwa osakwatira, ndi kwa akazi amasiye, kuti kuli bwino kwa iwo ngati akhala monganso ine. Koma ngati sadziwa kudziletsa, akwatitsidwe; pakuti nkwabwino kukwatira koposa kutentha mtima. Koma okwatitsidwawo ndiwalamulira, si ine ai, koma Ambuye, kuti mkazi asasiye mwamuna, komanso ngati amsiya akhale osakwatiwa, kapena ayanjanitsidwenso ndi mwamunayo, ndipo mwamuna asalekane naye mkazi. Koma kwa otsalawo ndinena ine, si Ambuye, Ngati mbale wina ali naye mkazi wosakhulupirira, ndipo iye avomera mtima kukhala naye pamodzi, asalekane naye. Ndipo mkazi amene ali naye mwamuna wosakhulupirira, navomera mtima iye kukhala naye pamodzi, asalekane naye mwamunayo. Pakuti mwamuna wosakhulupirirayo ayeretsedwa mwa mkaziyo, ndi mkazi wosakhulupirira ayeretsedwa mwa mbaleyo; ngati sikukadatero, ana anu akadakhala osakonzeka, koma tsopano akhala oyera. Koma ngati wosakhulupirirayo achoka, achoke. M'milandu yotere samangidwa ukapolo mbaleyo, kapena mlongoyo. Koma Mulungu watiitana ife mumtendere. Pakuti udziwa bwanji mkazi iwe, ngati udzapulumutsa mwamunayo? Kapena udziwa bwanji, mwamuna iwe, ngati udzapulumutsa mkazi? Koma, monga Ambuye wagawira kwa yense, monga Mulungu waitana yense, momwemo ayende. Ndipo kotero ndiika m'Mipingo yonse. Kodi waitanidwa wina wodulidwa? Asakhale wosadulidwa. Kodi waitanidwa wina wosadulidwa? Asadulidwe. Mdulidwe ulibe kanthu, ndi kusadulidwa kulibe kanthu, koma kusunga kwa malamulo a Mulungu. Yense akhale m'maitanidwe m'mene anaitanidwamo. Kodi unaitanidwa uli kapolo? Usasamalako; koma ngati ukhozanso kukhala mfulu, chita nako ndiko. Pakuti iye amene anaitanidwa mwa Ambuye, pokhala ali kapolo, ali mfulu ya Ambuye: momwemonso woitanidwayo, pokhala ali mfulu, ali kapolo wa Khristu. Munagulidwa ndi mtengo wake; musakhale akapolo a anthu. Yense, m'mene anaitanidwamo, abale, akhale momwemo ndi Mulungu. Koma kunena za anamwali, ndilibe lamulo la Ambuye; koma ndikuuzani choyesa iye, monga wolandira chifundo kwa Ambuye kukhala wokhulupirika. Chifukwa chake ndiyesa kuti ichi ndi chokoma chifukwa cha chivuto cha nyengo yino, kuti nkwabwino kwa munthu kukhala monga ali. Kodi wamangika kwa mkazi? Usafune kumasuka. Kodi wamasuka kwa mkazi? Usafune mkazi. Koma ungakhale ukwatira, sunachimwa; ndipo ngati namwali akwatiwa, sanachimwa. Koma otere adzakhala nacho chisautso m'thupi, ndipo ndikulekani. Koma ichi nditi, abale, yafupika nthawi, kuti tsopano iwo akukhala nao akazi akhalebe monga ngati alibe; ndi iwo akulira, monga ngati salira, ndi iwo akukondwera, monga ngati sakondwera; ndi iwo akugula monga ngati alibe kanthu; ndi iwo akuchita nalo dziko lapansi, monga ngati osachititsa; pakuti maonekedwe a dziko ili apita. Koma ndifuna kuti mukhale osalabadira. Iye amene wosakwatira alabadira zinthu za Ambuye, kuti akondweretse Ambuye; koma iye wokwatira alabadira zinthu za dziko lapansi, kuti akondweretse mkazi wake. Ndi mkazi wokwatiwa ndi namwali asiyananso. Iye wosakwatiwa alabadira za Ambuye, kuti akhale woyera m'thupi ndi mumzimu; koma wokwatiwayo, alabadira za dziko lapansi, kuti akondweretse mwamunayo. Koma ichi ndinena mwa kupindula kwanu kwa inu nokha; sikuti ndikakutchereni msampha, koma kukuthandizani kuchita chimene chiyenera, ndi kutsata chitsatire Ambuye, opanda chocheukitsa. Koma wina akayesa kuti achitira mwana wake wamkazi chosamuyenera, ngati palikupitirira pa unamwali wake, ndipo kukafunika kutero, achite chimene afuna, sachimwa; akwatitsidwe. Koma iye amene aima wokhazikika mumtima mwake, wopanda chikakamizo, koma ali nao ulamuliro wa pa chifuniro cha iye yekha, natsimikiza ichi mumtima mwa iye yekha, kusunga mwana wake wamkazi, adzachita bwino. Chotero iye amene akwatitsa mwana wake wamkazi achita bwino, ndipo iye wosamkwatitsa achita koposa. Mkazi amangika pokhala mwamuna wake ali ndi moyo; koma atamwalira mwamuna ali womasuka, kuti akwatiwe naye amene afuna, koma mwa Ambuye. Koma akhala wokondwera koposa ngati akhala monga momwe ali, monga mwa kuyesa kwanga; ndipo ndinagiza kuti inenso ndili naye Mzimu wa Mulungu. Koma za zoperekedwa nsembe kwa mafano: Tidziwa kuti tili nacho chidziwitso tonse. Chidziwitso chitukumula, koma chikondi chimangirira. Ngati wina ayesa kuti adziwa kanthu sanayambe kudziwa monga ayenera kudziwa. Koma ngati wina akonda Mulungu, yemweyu adziwika ndi Iye. Tsono kunena za kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano, tidziwa kuti fano silili kanthu pa dziko lapansi, ndi kuti palibe Mulungu koma mmodzi. Pakuti ngakhalenso iliko yoti yonenedwa milungu, kapena m'mwamba, kapena pa dziko lapansi, monga iliko milungu yambiri, ndi ambuye ambiri; koma kwa ife kuli Mulungu mmodzi, Atate amene zinthu zonse zichokera kwa Iye, ndi ife kufikira kwa Iye; ndi Ambuye mmodzi Yesu Khristu, amene zinthu zonse zili mwa Iye, ndi ife mwa Iye. Komatu chidziwitso sichili mwa onse; koma ena, ozolowera fano kufikira tsopano, adyako monga yoperekedwa nsembe kwa fano; ndipo chikumbu mtima chao, popeza nchofooka, chidetsedwa. Koma chakudya sichitivomerezetsa kwa Mulungu; kapena ngati sitidya sitisowa; kapena ngati tidya tilibe kupindulako. Koma yang'anirani kuti ulamuliro wanu umene ungakhale chokhumudwitsa ofookawo. Pakuti wina akaona iwe amene uli nacho chidziwitso, ulikukhala pachakudya m'Kachisi wa fano, kodi chikumbu mtima chake, popeza ali wofooka, sichidzalimbika kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano? Pakuti mwa chidziwitso chako wofookayo atayika, ndiye mbale amene Khristu anamfera. Koma pakuchimwira abale, ndi kulasa chikumbu mtima chao chofooka, muchimwira kotero Khristu. Chifukwa chake, ngati chakudya chikhumudwitsa mbale wanga, sindidzadya nyama kunthawi yonse, kuti ndingakhumudwitse mbale wanga. Kodi sindine mfulu? Kodi sindine mtumwi? Kodi sindinaona Yesu Ambuye wathu? Kodi simuli inu ntchito yanga mwa Ambuye? Ngati sindili mtumwi kwa ena, komatu ndili kwa inu; pakuti chizindikiro cha utumwi wanga ndi inu mwa Ambuye. Chodzikanira changa kwa iwo amene andifunsa ine ndi ichi: Kodi tilibe ulamuliro wa kudya ndi kumwa? Kodi tilibe ulamuliro wakuyendayenda naye mkazi, ndiye mbale, monganso atumwi ena, ndi abale a Ambuye, ndi Kefa? Kapena kodi ife tokha, Barnabasi ndi ine tilibe ulamuliro wakusagwira ntchito? Msilikali ndani achita nkhondo, nthawi iliyonse, nadzifunira zake yekha? Aoka mipesa ndani, osadya chipatso chake? Kapena aweta gulu ndani, osadya mkaka wake wa gululo? Kodi ndilankhula izi monga mwa anthu? Kapena chilamulo sichinenanso zomwezo? Pakuti m'chilamulo cha Mose mwalembedwa, Usapunamitsa ng'ombe pakupuntha iyo dzinthu. Kodi Mulungu asamalira ng'ombe? Kapena achinena ichi konsekonse chifukwa cha ife? Pakuti, chifukwa cha ife kwalembedwa: popeza wolima ayenera kulima mwa chiyembekezo, ndi wopunthayo achita mwa chiyembekezo cha kugawana nao. Ngati takufeserani inu zauzimu, kodi nchachikulu ngati ife tituta za thupi lanu? Ngati ena ali nao ulamuliro umene pa inu, si ife nanga koposa? Koma sitinachita nao ulamuliro umene; koma timalola zonse, kuti tingachite chochedwetsa kwa Uthenga Wabwino wa Khristu. Kodi simudziwa kuti iwo akutumikira za Kachisi amadya za m'Kachisi, ndi iwo akuimirira guwa la nsembe, agawana nalo guwa la nsembe? Chomwechonso Ambuye analamulira kuti iwo amene alalikira Uthenga Wabwino akhale ndi moyo ndi Uthenga Wabwino. Koma ine sindinachita nako kanthu ka izi; ndipo sindilemba izi kuti chikakhale chotero ndi ine; pakuti kundikomera ine kufa, koma wina asayese kwachabe kudzitamanda kwanga. Pakuti ngati ndilalikira Uthenga Wabwino ndilibe kanthu kakudzitamandira; pakuti chondikakamiza ndigwidwa nacho; pakuti tsoka ine ngati sindilalikira Uthenga Wabwino. Pakuti ngati ndichita ichi chivomerere, mphotho ndili nayo; koma ngati si chivomerere, anandikhulupirira m'udindo. Mphotho yanga nchiyani tsono? Kuti pakulalikira Uthenga Wabwino ndiyese Uthenga Wabwino ukhale waulere, kuti ndisaipse ulamuliro wanga wa mu Uthenga Wabwino. Pakuti pokhala ndinali mfulu kwa onse, ndinadzilowetsa ndekha ukapolo kwa onse, kuti ndipindule ochuluka. Ndipo kwa Ayuda ndinakhala monga Myuda, kuti ndipindule Ayuda; kwa iwo omvera lamulo monga womvera lamulo, ngakhale sindinakhala ndekha womvera lamulo, kuti ndipindule iwo omvera malamulo; kwa iwo opanda lamulo monga wopanda lamulo, wosati wakukhala ine wopanda lamulo kwa Mulungu, koma womvera lamulo kwa Khristu kuti ndipindule iwo opanda lamulo. Kwa ofooka ndinakhala ngati wofooka, kuti ndipindule ofooka. Ndakhala zonse kwa anthu onse, kuti paliponse ndikapulumutse ena. Koma ndichita zonse chifukwa cha Uthenga Wabwino, kuti ndikakhale woyanjana nao. Kodi simudziwa kuti iwo akuchita makani a liwiro, athamangadi onse, koma mmodzi alandira mfupo? Motero thamangani, kuti mukalandire. Koma yense wakuyesetsana adzikanizira zonse. Ndipo iwowa atero kuti alandire korona wakuvunda; koma ife wosavunda. Chifukwa chake ine ndithamanga chotero, si monga chosinkhasinkha. Ndilimbana chotero, si monga ngati kupanda mlengalenga; koma ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha. Pakuti sindifuna, kuti mukhale osadziwa, abale, kuti makolo athu onse anali pansi pa mtambo, naoloka nyanja onse; nabatizidwa onse kwa Mose, mumtambo, ndi m'nyanja, nadya onse chakudya chauzimu chimodzimodzi; namwa onse chakumwa chauzimu chimodzimodzi; pakuti anamwa mwa thanthwe lauzimu lakuwatsata; koma thanthwelo ndiye Khristu. Koma ochuluka a iwo Mulungu sanakondwera nao; pakuti anamwazika m'chipululu. Koma zinthu izi zinachitika, zikhale zotichenjeza ife, kuti tisalakalake zoipa ife, monganso iwowo analakalaka. Kapena musakhale opembedza mafano, monga ena a iwo, monga kwalembedwa, Anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nanyamuka kusewera. Kapena tisachite dama monga ena a iwo anachita dama, nagwa tsiku limodzi zikwi makumi awiri ndi zitatu. Kapena tisayese Ambuye, monga ena a iwo anayesa, naonongeka ndi njoka zija. Kapena musadandaula, monga ena a iwo anadandaula, naonongeka ndi woonongayo. Koma izi zinachitika kwa iwowa monga zotichenjeza, ndipo zinalembedwa kutichenjeza ife, amene matsirizidwe a nthawi ya pansi pano adafika pa ife. Chifukwa chake iye wakuyesa kuti ali chilili, ayang'anire kuti angagwe. Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako. Chifukwa chake, okondedwa anga, thawani kupembedza mafano. Ndinena monga kwa anzeru; lingirirani inu chimene ndinena. Chikho cha dalitso chimene tidalitsa, sichili chiyanjano cha mwazi wa Khristu kodi? Mkate umene tinyema suli chiyanjano cha thupi la Khristu kodi? Pakuti mkate ndiwo umodzi, chotero ife ambiri ndife thupi limodzi; pakuti ife tonse titengako kumkate umodzi. Tapenyani Israele monga mwa thupi; kodi iwo akudya nsembezo alibe chiyanjano ndi guwa la nsembe? Ndinena chiyani tsono? Kuti choperekedwa nsembe kwa mafano chili kanthu? Kapena kuti fano lili kanthu kodi? Koma nditi kuti zimene amitundu apereka nsembe azipereka kwa ziwanda osati kwa Mulungu; ndipo sindifuna kuti inu muyanjane ndi ziwanda. Simungathe kumwera chikho cha Ambuye, ndi chikho cha ziwanda; simungathe kulandirako kugome la Ambuye, ndi kugome la ziwanda. Kapena kodi tichititsa nsanje Ambuye? Kodi mphamvu zathu ziposa Iye? Zinthu zonse ziloleka; koma sizipindula zonse. Zinthu zonse ziloleka; koma sizimanga zonse. Munthu asafune zake za iye yekha, koma za mnzake. Chonse chogulitsidwa pa msika wa nyama, mudye, osafunsa kanthu chifukwa cha chikumbu mtima; pakuti dziko lapansi lili la Ambuye, ndi kudzala kwake. Ngati wina wa osakhulupirira akuitanani, ndipo mufuna kupita; mudye chomwe chiikidwa kwa inu, osafunsa kanthu, chifukwa cha chikumbu mtima. Koma ngati wina akati kwa inu, Yoperekedwa nsembe iyi, musadye, chifukwa cha iyeyo wakuuza, ndi chifukwa cha chikumbu mtima. Ndinena chikumbu mtima, si cha iwe mwini, koma cha winayo; pakuti ufulu wanga uyesedwa ninji ndi chikumbu mtima cha wina? Ngati ine ndilandirako mwachisomo, ndinenezedwa bwanji chifukwa cha ichi chimene ndiyamikapo? Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu. Khalani osakhumudwitsa, kapena Ayuda, kapena Agriki, kapena Mpingo wa Mulungu; monga inenso ndikondweretsa onse m'zinthu zonse, wosafuna chipindulo changa, koma cha unyunjiwo, kuti apulumutsidwe. Khalani onditsanza ine, monga inenso nditsanza Khristu. Ndipo ndikutamandani kuti m'zinthu zonse mukumbukira ine, ndi kuti musunga miyambo monga ndinapereka kwa inu. Koma ndifuna kuti mudziwe, kuti mutu wa munthu yense ndiye Khristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu. Mwamuna yense woveka mutu, popemphera kapena ponenera, anyoza mutu wake. Koma mkazi yense wakupemphera, kapena kunenera, wovula mutu, anyoza mutu wake; pakuti kuli chimodzimodzi kumetedwa. Pakuti ngati mkazi safunda, asengedwenso; koma ngati kusengedwa kapena kumetedwa kuchititsa manyazi, afunde. Pakuti mwamuna sayenera kuvala pamutu, popeza akhala fanizo ndi ulemerero wa Mulungu: koma mkazi ali ulemerero wa mwamuna. Pakuti mwamuna sakhala wa kwa mkazi; koma mkazi wa kwa mwamuna; pakutinso mwamuna sanalengedwa chifukwa cha mkazi; koma mkazi chifukwa cha mwamuna; chifukwa cha ichi mkazi ayenera kukhala nao ulamuliro pamutu pake, chifukwa cha angelo. Komanso mkazi sakhala wopanda mwamuna, kapena mwamuna wopanda mkazi, mwa Ambuye. Pakuti monga mkazi ali wa kwa mwamuna, chomwechonso mwamuna ali mwa mkazi; koma zinthu zonse zili za kwa Mulungu. Lingirirani mwa inu nokha: Kodi nkuyenera kuti apemphere kwa Mulungu, wosafunda mutu? Kodi ubadwidwe womwe sutiphunzitsa kuti ngati mwamuna aweta tsitsi chinyozetsa iye? Koma ngati mkazi aweta tsitsi, kuli ulemerero kwa iye; pakuti tsitsi lake lapatsidwa kwa iye ngati chophimba. Koma akaoneka wina ngati wotetana, tilibe makhalidwe otere, kapena ife, kapena Mpingo wa Mulungu. Koma pakulalikira ichi sinditama inu, popeza simusonkhanira chokoma, koma choipa. Pakutitu poyamba posonkhana inu mu Mpingo, ndimva kuti pakhala malekano mwa inu; ndipo ndivomereza penapo. Pakuti kuyenera kuti pakhale mipatuko mwa inu, kuti iwo ovomerezedwa aonetsedwe mwa inu. Chifukwa chake, pakusonkhana inu pamodzi sikutheka kudya mgonero wa Ambuye; pakuti pakudyaku yense athanga watenga mgonero wake wa yekha, ndipo wina ali ndi njala, ndi wina aledzera. Nanga mulibe nyumba za kudyeramo ndi kumweramo? Kapena kodi munyoza Mpingo wa Mulungu, ndi kunyoza iwo amene alibe kanthu? Ndidzanena chiyani kwa inu? Kodi ndidzatama inu m'menemo? Sindikutamani. Pakuti ine ndinalandira kwa Ambuye, chimenenso ndinapereka kwa inu, kuti Ambuye Yesu usiku uja anaperekedwa, anatenga mkate; ndipo m'mene adayamika, ananyema, nati, Ichi ndi thupi langa la kwa inu; chitani ichi chikhale chikumbukiro changa. Koteronso chikho, chitatha chakudya, ndi kuti, Chikho ichi ndi pangano latsopano m'mwazi wanga; chitani ichi, nthawi zonse mukamwa, chikhale chikumbukiro changa. Pakuti nthawi zonse mukadya mkate uwu ndi kumwera chikho, mulalikira imfa ya Ambuye kufikira akadza Iye. Chifukwa chake yense amene akadya mkate, kapena akamwera chikho cha Ambuye kosayenera, adzakhala wochimwira thupi ndi mwazi wa Ambuye. Koma munthu adziyese yekha, ndi kotero adye mkate, ndi kumwera chikho. Pakuti iye wakudya ndi wakumwa, adya namwa chiweruziro kwa iye yekha, ngati sazindikira thupilo. Chifukwa chake ambiri mwa inu afooka, nadwala, ndipo ambiri agona. Koma ngati tikadadzizindikira tokha sitikadaweruzidwa. Koma poweruzidwa, tilangidwa ndi Ambuye, kuti tingatsutsidwe pamodzi ndi dziko lapansi. Chifukwa chake, abale anga, posonkhanira kudya, lindanani. Ngati wina ali ndi njala adye kwao; kuti mungasonkhanire kwa chiweruziro. Koma zotsalazo ndidzafotokoza pakudza ine. Koma za mphatso zauzimu, abale, sindifuna kuti mukhale osadziwa. Mudziwa kuti pamene munali amitundu, munatengedwa kunka kwa mafano aja osalankhula, monga munatsogozedwa. Chifukwa chake ndikuuzani inu, kuti palibe munthu wakulankhula mwa Mzimu wa Mulungu, anena, Yesu ngwotembereredwa; ndipo palibe wina akhoza kunena, Yesu ali Ambuye, koma mwa Mzimu Woyera. Ndipo pali mphatso zosiyana, koma Mzimu yemweyo. Ndipo pali mautumiki osiyana, koma Ambuye yemweyo. Ndipo pali machitidwe osiyana, koma Mulungu yemweyo, wakuchita zinthu zonse mwa onse. Koma kwa yense kwapatsidwa maonekedwe a Mzimu kuti apindule nao. Pakuti kwa mmodzi kwapatsidwa mwa Mzimu mau a nzeru; koma kwa mnzake mau a chidziwitso, monga mwa Mzimu yemweyo: kwa wina chikhulupiriro, mwa Mzimu yemweyo; ndi kwa wina mphatso za machiritso, mwa Mzimu mmodziyo; ndi kwa wina machitidwe a mphamvu; ndi kwa wina chinenero; ndi kwa wina chizindikiro cha mizimu; kwa wina malilime a mitundumitundu; ndi kwa wina mamasulidwe a malilime. Koma zonse izi achita Mzimu mmodzi yemweyo, nagawira yense pa yekha monga afuna. Pakuti monga thupi lili limodzi, nilikhala nazo ziwalo zambiri; koma ziwalo zonse za thupilo, pokhala zambiri, zili thupi limodzi; momwemonso Khristu. Pakutinso mwa Mzimu mmodzi ife tonse tinabatizidwa kulowa m'thupi limodzi, ngakhale Ayuda, ngakhale Agriki, ngakhale akapolo, ngakhale mfulu; ndipo tonse tinamwetsedwa Mzimu mmodzi. Pakutinso thupi silikhala chiwalo chimodzi, koma zambiri. Ngati phazi likati, Popeza sindili dzanja, sindili wa thupi; kodi silili la thupi chifukwa cha ichi? Ndipo ngati khutu likati, Popeza sindili diso, sindili wa thupi; kodi silili la thupi chifukwa cha ichi? Ngati thupi lonse likadakhala diso, kukadakhala kuti kununkhiza? Koma tsopano, Mulungu anaika ziwalo zonsezo m'thupi, monga anafuna. Koma ngati zonse zikadakhala chiwalo chimodzi, likadakhala kuti thupi? Koma tsopano pali ziwalo zambiri, koma thupi limodzi. Ndipo diso silingathe kunena kwa dzanja, Sindikufuna iwe, kapenanso mutu kwa mapazi, Sindikufunani inu. Koma makamakatu ziwalozo zoyesedwa zofooka m'thupi, zifunika; ndipo zimene tiziyesa zochepa ulemu m'thupi, pa izi tiika ulemu wochuluka woposa; ndi zinthu zosakoma zikhala nacho chokometsera choposa. Koma zokoma zathu zilibe kusowa; koma Mulungu analumikizitsa thupi, napatsa ulemu wochuluka kwa chosowacho; kuti kusakhale chisiyano m'thupi; koma kuti ziwalo zifanane ndi kusamalana china ndi chinzake. Ndipo chingakhale chiwalo chimodzi chimva chowawa, ziwalo zonse zimva pamodzi; chingakhale chimodzi chilemekezedwa, ziwalo zonse zikondwera nacho pamodzi. Koma inu ndinu thupi la Khristu, ndi ziwalo, yense pa yekha. Ndipotu Mulungu anaika ena mu Mpingo, poyamba atumwi, achiwiri aneneri, achitatu aphunzitsi, pamenepo zozizwa, pomwepo mphatso za machiritso, mathandizo, maweruziro, malilime a mitundumitundu. Kodi ali onse atumwi? Ali aneneri onse kodi? Ali aphunzitsi onse? Ali onse ochita zozizwa? Ali nazo mphatso za machiritso onse kodi? Kodi onse alankhula ndi malilime? Kodi onse amasulira mau? Koma funitsitsani mphatso zoposa. Ndipo ndikuonetsani njira yokoma yoposatu. Ndingakhale ndilankhula malilime a anthu, ndi a angelo, koma ndilibe chikondi, ndikhala mkuwa woomba, kapena nguli yolira. Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndili nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndilibe chikondi, ndili chabe. Ndipo ndingakhale ndipereka chuma changa chonse kudyetsa osauka, ndipo ndingakhale ndipereka thupi langa alitenthe m'moto, koma ndilibe chikondi, sindipindula kanthu ai. Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziwa kudzitamanda, sichidzikuza, sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima, sichilingirira zoipa; sichikondwera ndi chinyengo, koma chikondwera ndi choonadi; chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse. Chikondi sichitha nthawi zonse, koma kapena zonenera zidzakhala chabe, kapena malilime adzaleka, kapena nzeru idzakhala chabe. Pakuti ife tidziwa mderamdera, ndimo tinenera mderamdera. Koma pamene changwiro chafika, tsono chamderamdera chidzakhala chabe. Pamene ndinali mwana, ndinalankhula ngati mwana, ndinalingirira ngati mwana, ndinawerenga ngati mwana; tsopano ndakhala munthu, ndayesa chabe zachibwana. Pakuti tsopano tipenya m'kalirole, ngati chimbuuzi; koma pomwepo maso ndi maso. Tsopano ndizindikira mderamdera; koma pomwepo ndidzazindikiratu, monganso ndazindikiridwa. Ndipo tsopano zitsala chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi, zitatu izi; koma chachikulu cha izi ndicho chikondi. Tsatani chikondi; koma funitsitsani mphatso zauzimu, koma koposa kuti mukanenere. Pakuti iye wakulankhula lilime salankhula ndi anthu, koma ndi Mulungu; pakuti palibe munthu akumva; koma mumzimu alankhula zinsinsi. Koma iye wakunenera alankhula ndi anthu chomangirira ndi cholimbikitsa, ndi chosangalatsa. Iye wakulankhula lilime, adzimangirira yekha, koma iye wakunenera amangirira Mpingo. Ndipo ndifuna inu nonse mulankhule malilime, koma makamaka kuti mukanenere; ndipo wakunenera aposa wakulankhula malilime, akapanda kumasulira, kuti Mpingo ukalandire chomangirira. Koma tsopano, abale, ngati ndidza kwa inu ndi kulankhula malilime, ndikakupindulitsani chiyani, ngati sindilankhula ndi inu kapena m'vumbulutso, kapena m'chidziwitso, kapena m'chinenero, kapena m'chiphunzitso? Ngakhale zinthu zopanda moyo, zopereka mau, ngati chitoliro, kapena ngoli, ngati sizisiyanitsa maliridwe, chidzazindikirika bwanji chimene chiombedwa kapena kuimbidwa? Pakuti ngati lipenga lipereka mau osazindikirika, adzadzikonzera ndani kunkhondo? Momwemonso inu ngati mwa lilime simupereka mau omveka bwino, kudzazindikirika bwanji chimene chilankhulidwa? Pakuti mudzakhala olankhula kumlengalenga. Ilipo, kaya, mitundu yambiri yotere ya mau pa dziko lapansi, ndipo palibe kanthu kasowa mau. Chifukwa chake, ngati sindidziwa mphamvu ya mauwo ndidzakhala kwa iye wolankhulayo wakunja, ndipo wolankhulayo adzakhala wakunja kwa ine. Momwemo inunso, popeza muli ofunitsitsa mphatso za Mzimu, funani kuti mukachuluke kukumangirira kwa Mpingo. Chifukwa chake wolankhula lilime, apemphere kuti amasule. Pakuti ngati ndipemphera m'lilime, mzimu wanga upemphera, koma chidziwitso changa chikhala chosabala kanthu. Kuli chiyani tsono? Ndidzapemphera ndi mzimu, koma ndidzapempheranso ndi chidziwitso changa; ndidzaimba ndi mzimu, koma ndidzaimbanso ndi chidziwitso. Chifukwa ngati udalitsa ndi mzimu, nanga iye wakukhala wosaphunzira adzati Amen bwanji, pa kuyamika kwako, popeza sadziwa chimene unena? Pakutitu iwe uyamika bwino, koma winayo samangiriridwa. Ndiyamika Mulungu kuti ndilankhula malilime koposa inu nonse; koma mu Mpingo ndifuna kulankhula mau asanu ndi zidziwitso changa, kutinso ndikalangize ena, koposa kulankhula mau zikwi m'lilime. Abale, musakhale ana m'chidziwitso, koma m'choipa khalani makanda, koma m'chidziwitso akulu misinkhu. Kwalembedwa m'chilamulo, Ndi anthu a malilime ena ndipo ndi milomo ina ndidzalankhula nao anthu awa; ndipo kungakhale kutero sadzamva Ine, anena Ambuye. Chotero malilime akhala ngati chizindikiro, si kwa iwo akukhulupirira, koma kwa iwo osakhulupirira; koma kunenera sikuli kwa iwo osakhulupirira, koma kwa iwo amene akhulupirira. Chifukwa chake, ngati Mpingo wonse akasonkhane pamodzi, ndi onse akalankhule malilime, ndipo akalowemo anthu osaphunzira kapena osakhulupirira, kodi sadzanena kuti mwayaluka? Koma ngati onse anenera, ndipo alowamo wina wosakhulupirira kapena wosaphunzira, atsutsidwa ndi onse; aweruzidwa ndi onse; zobisika za mtima wake zionetsedwa; ndipo chotero adzagwa nkhope yake pansi, nadzagwadira Mulungu, nadzalalikira kuti Mulungu ali ndithu mwa inu. Nanga chiyani tsono, abale? Pamene musonkhana, yense ali nalo salimo, ali nacho chiphunzitso, ali nalo vumbulutso, ali nalo lilime, ali nacho chimasuliro. Muchite zonse kukumangirira. Ngati wina alankhula lilime, achite ndi awiri, koma oposa atatu iai, ndipo motsatana; ndipo mmodzi amasulire. Koma ngati palibe womasulira, akhale chete mu Mpingo, koma alankhule ndi iye yekha, ndi Mulungu. Ndipo aneneri alankhule awiri kapena atatu, ndi ena azindikire. Koma ngati kanthu kuvumbulutsidwa kwa wina wakukhalapo, akhale chete woyambayo. Pakuti mukhoza nonse kunenera mmodzimmodzi, kuti onse aphunzire, ndi onse afulumidwe; ndipo mizimu ya aneneri imvera aneneri; pakuti Mulungu sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere; monga mwa Mipingo yonse ya oyera mtima. Akazi akhale chete m'Mipingo. Pakuti sikuloledwa kwa iwo kulankhula. Koma akhale omvera, monganso chilamulo chinena. Koma ngati afuna kuphunzira kanthu afunse amuna ao a iwo okha kwao; pakuti kunyazitsa mkazi kulankhula mu Mpingo. Kodi mau a Mulungu anatuluka kwa inu? Kapena anafika kwa inu nokha? Ngati wina ayesa kuti ali mneneri, kapena wauzimu, azindikire kuti zimene ndilemba kwa inu zili lamulo la Ambuye. Koma ngati wina akhale wosadziwa, akhale wosadziwa. Chifukwa chake, abale anga, funitsitsani kunenera, ndipo musaletse kulankhula malilime. Koma zonse zichitike koyenera ndi kolongosoka. Ndipo ndikudziwitsani, abale, Uthenga Wabwino umene ndinakulalikirani inu, umenenso munalandira, umenenso muimamo, umenenso mupulumutsidwa nao ngati muugwiritsa monga momwe ndinalalikira kwa inu; ngati simunakhulupirira chabe. Pakuti ndinapereka kwa inu poyamba, chimenenso ndinalandira, kuti Khristu anafera zoipa zathu, monga mwa malembo; ndi kuti anaikidwa; ndi kuti anaukitsidwa tsiku lachitatu, monga mwa malembo; ndi kuti anaonekera kwa Kefa; pamenepo kwa khumi ndi awiriwo; pomwepo anaoneka pa nthawi imodzi kwa abale oposa mazana asanu, amene ochuluka a iwo akhala kufikira tsopano, koma ena agona; pomwepo anaonekera kwa Yakobo; pamenepo kwa atumwi onse; ndipo potsiriza pake pa onse, anaoneka kwa inenso monga mtayo. Pakuti ine ndili wamng'ono wa atumwi, ndine wosayenera kutchedwa mtumwi, popeza ndinalondalonda Mpingo wa Mulungu. Koma ndi chisomo cha Mulungu ndili ine amene ndili; ndipo chisomo chake cha kwa ine sichinakhala chopanda pake, koma ndinagwirira ntchito yochuluka ya iwo onse; koma si ine, koma chisomo cha Mulungu chakukhala ndi ine. Ngati ine tsono, kapena iwowa, kotero tilalikira, ndi kotero munakhulupirira. Koma ngati Khristu alalikidwa kuti waukitsidwa kwa akufa, nanga ena mwa inu anena bwanji kuti kulibe kuuka kwa akufa? Koma ngati kulibe kuuka kwa akufa, Khristunso sanaukitsidwa; ndipo ngati Khristu sanaukitsidwa kulalikira kwathu kuli chabe, chikhulupiriro chanunso chili chabe. Ndiponso ife tipezedwa mboni zonama za Mulungu; chifukwa tinachita umboni kunena za Mulungu kuti anaukitsa Khristu; amene sanamuukitsa, ngati kuli tero kuti akufa saukitsidwa. Pakuti ngati akufa saukitsidwa, Khristunso sanaukitsidwa; ndipo ngati Khristu sanaukitsidwa, chikhulupiriro chanu chili chopanda pake; muli chikhalire m'machimo anu. Chifukwa chake iwonso akugona mwa Khristu anatayika. Ngati tiyembekezera Khristu m'moyo uno wokha, tili ife aumphawi oposa a anthu onse. Koma tsopano Khristu waukitsidwa kwa akufa, chipatso choundukula cha iwo akugona. Pakuti monga imfa inadza mwa munthu, kuuka kwa akufa kunadzanso mwa munthu. Pakuti monga mwa Adamu onse amwalira, choteronso mwa Khristu onse akhalitsidwa ndi moyo. Koma yense m'dongosolo lake la iye yekha, chipatso choundukula Khristu; pomwepo iwo a Khristu, pakubwera kwake. Pomwepo pali chimaliziro, pamene adzapereka ufumu kwa Mulungu, ndiye Atate, atatha kuthera chiweruzo chonse, ndi ulamuliro wonse, ndi mphamvu yomwe. Pakuti ayenera kuchita ufumu kufikira ataika adani onse pansi pa mapazi ake. Mdani wotsiriza amene adzathedwa ndiye imfa. Pakuti Iye anagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake. Koma pamene anena kuti zonse zagonjetsedwa, kuzindikirika kuti sawerengapo Iye amene anagonjetsa zonsezo kwa Iye. Ndipo pamene zonsezo zagonjetsedwa kwa Iye, pomwepo Mwana yemwe adzagonjetsedwa kwa Iye amene anamgonjetsera zinthu zonse, kuti Mulungu akhale zonse mu zonse. Ngati si kutero, adzachita chiyani iwo amene abatizidwa chifukwa cha akufa? Ngati akufa saukitsidwa konse, abatizidwa chifukwa ninji chifukwa cha iwo? Nanga ifenso tili m'moopsa bwanji nthawi zonse? Ndifa tsiku ndi tsiku, ndilumbira pa kudzitamandira kwa inu, abale, kumene ndili nako mwa Khristu Yesu, Ambuye wathu. Ngati ndinalimbana ndi zilombo ku Efeso monga mwa munthu, ndipindulanji? Ngati akufa saukitsidwa, tidye timwe pakuti mawa timwalira. Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma. Ukani molungama, ndipo musachimwe; pakuti ena alibe chidziwitso cha Mulungu. Ndilankhula kunyaza inu. Koma wina adzati, Akufa aukitsidwa bwanji? Ndipo adza nalo thupi lotani? Wopusa iwe, chimene uchifesa wekha sichikhalitsidwanso chamoyo, ngati sichifa; ndipo chimene ufesa, sufesa thupi limene lidzakhala, koma mbeu yokha kapena ya tirigu kapena ya mtundu wina; koma Mulungu aipatsa thupi monga afuna; ndi kwa mbeu yonse thupi lakelake. Nyama yonse siili imodzimodzi; koma ina ndi ya anthu, ndi ina ndiyo nyama ya zoweta, ndi ina ndiyo nyama ya mbalame, ndi ina ya nsomba. Palinso matupi am'mwamba, ndi matupi apadziko: koma ulemerero wa lam'mwamba ndi wina, ndi ulemerero wa lapadziko ndi winanso. Kuli ulemerero wa dzuwa, ndi ulemerero wina wa mwezi, ndi ulemerero wina wa nyenyezi; pakuti nyenyezi isiyana ndi nyenyezi m'ulemerero. Chomwechonso kudzakhala kuuka kwa akufa. Lifesedwa m'chivundi, liukitsidwa m'chisavundi; lifesedwa m'mnyozo, liukitsidwa m'ulemerero; lifesedwa m'chifooko, liukitsidwa mumphamvu; lifesedwa thupi lachibadwidwe, liukitsidwa thupi lauzimu. Ngati pali thupi lachibadwidwe, palinso lauzimu. Koteronso kwalembedwa, Munthu woyamba, Adamu, anakhala mzimu wamoyo. Adamu wotsirizayo anakhala mzimu wakulenga moyo. Koma chauzimu sichili choyamba, koma chachibadwidwe; pamenepo chauzimu. Munthu woyambayo ali wapansi, wanthaka. Munthu wachiwiri ali wakumwamba. Monga wanthakayo, ateronso anthaka; ndi monga wakumwamba, ateronso akumwamba. Ndipo monga tavala fanizo la wanthakayo, tidzavalanso fanizo la wakumwambayo. Koma ndinena ichi, abale, kuti thupi ndi mwazi sizingathe kulowa Ufumu wa Mulungu; kapena chivundi sichilowa chisavundi. Taonani, ndikuuzani chinsinsi; sitidzagona tonse, koma tonse tidzasandulika, m'kamphindi, m'kuthwanima kwa diso, pa lipenga lotsiriza; pakuti lipenga lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa osavunda, ndipo ife tidzasandulika. Pakuti chovunda ichi chiyenera kuvala chisavundi, ndi chaimfa ichi kuvala chosafa. Ndipo pamene chovunda ichi chikadzavala chisavundi ndi chaimfa ichi chikadzavala chosafa, pamenepo padzachitika mau olembedwa, Imfayo yamezedwa m'chigonjetso. Imfawe, chigonjetso chako chili kuti? Imfawe, mbola yako ili kuti? Koma mbola ya imfa ndiyo uchimo; koma mphamvu ya uchimo ndiyo chilamulo: koma ayamikike Mulungu, amene atipatsa ife chigonjetso mwa Ambuye wathu Yesu Khristu. Chifukwa chake, abale anga okondedwa, khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye. Koma za chopereka cha kwa oyera mtima, monga ndinalangiza Mipingo ya ku Galatiya, motero chitani inunso. Tsiku loyamba la sabata yense wa inu asunge yekha, monga momwe anapindula, kuti zopereka zisachitike pakudza ine. Ndipo pamene ndifika, ndidzatuma iwo amene mudzawayesa oyenera, ndi akalata, apite nayo mphatso yanu ku Yerusalemu. Ndipo ngati kuyenera kwa ine kupitanso, adzapita nane. Koma ndidzadza kwa inu, nditapyola Masedoniya; pakuti ndidzapyola Masedoniya; ndipo kapena ndidzakhalitsa ndi inu, kapenanso kugonera nyengo yachisanu kuti mukandiperekeze ine kumene kulikonse ndipitako. Pakuti sindifuna kukuonani tsopano popitirira; pakuti ndiyembekeza kukhala ndi inu nthawi, ngati alola Ambuye. Koma ndidzakhala ku Efeso kufikira Pentekoste. Pakuti panditsegukira pa khomo lalikulu ndi lochititsa, ndipo oletsana nafe ndi ambiri. Koma akadza Timoteo, penyani kuti akhale ndi inu wopanda mantha; pakuti agwira ntchito ya Ambuye, monganso ine; chifukwa chake munthu asampeputse. Koma mumperekeze mumtendere, kuti akadze kwa ine; pakuti ndimuyembekezera pamodzi ndi abale. Koma za Apolo, mbaleyo, ndamuumiriza iye, adze kwa inu pamodzi ndi abale; ndipo sichinali chifuniro chake kuti adze tsopano, koma adzafika pamene aona nthawi. Dikirani, chilimikani m'chikhulupiriro, dzikhalitseni amuna, limbikani. Zanu zonse zichitike m'chikondi. Koma ndikupemphani inu, abale, (mudziwa banja la Stefanasi, kuti ali chipatso choundukula cha Akaya, ndi kuti anadziika okha kutumikira oyera mtima), kuti inunso muvomere otere, ndi yense wakuchita nao, ndi kugwiritsa ntchito. Koma ndikondwera pa kudza kwao kwa Stefanasi, ndi Fortunato, ndi Akaiko; chifukwa iwo anandikwaniritsa chotsalira chanu. Pakuti anatsitsimutsa mzimu wanga ndi wanu; chifukwa chake muzindikire otere. Mipingo ya ku Asiya ikupatsani moni. Akupatsani moni ndithu inu mwa Ambuye, Akwila ndi Prisika, pamodzi ndi Mpingo wa m'nyumba yao. Akupatsani moni abale onse. Mupatsane moni ndi kupsompsona kopatulika. Ndikupereka moni ine Paulo ndi dzanja langa. Ngati wina sakonda Ambuye, akhale wotembereredwa. Akudza Ambuye. Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu chikhale ndi inu. Chikondi changa chikhale ndi inu nonse mwa Khristu Yesu. Amen. Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu, mwa chifuniro cha Mulungu, ndi Timoteo mbaleyo, kwa Mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto, pamodzi ndi oyera mtima onse amene ali m'Akaya monse: Chisomo kwa inu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu. Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse, wotitonthoza ife m'nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m'nsautso iliyonse, mwa chitonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu. Pakuti monga masautso a Khristu atichulukira ife, choteronso chitonthozo chathu chichuluka mwa Khristu. Koma ngati tisautsidwa, kuli chifukwa cha chitonthozo ndi chipulumutso chanu; ngati titonthozedwa, kuli kwa chitonthozo chanu chimene chichititsa mwa kupirira kwa masautso omwewo amene ifenso timva. Ndipo chiyembekezo chathu cha kwa inu nchokhazikika; podziwa kuti monga muli oyanjana ndi masautsowo, koteronso ndi chitonthozo. Pakuti sitifuna abale, kuti mukhale osadziwa za chisautso chathu tinakomana nacho m'Asiya, kuti tinathodwa kwakukulu, koposa mphamvu yathu, kotero kuti tinada nkhawa ngakhale za moyo wathu; koma tokha tinakhala nacho chitsutso cha imfa mwa ife tokha, kuti tisalimbike pa ife tokha, koma pa Mulungu wakuukitsa akufa; amene anatilanditsa mu imfa yaikulu yotere, nadzalanditsa; amene timyembekezera kuti adzalanditsanso; pothandizana inunso ndi pemphero lanu la kwa ife; kuti pa mphatso ya kwa ife yodzera kwa anthu ambiri, payamikike ndi anthu ambiri chifukwa cha ife. Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbu mtima chathu, kuti m'chiyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'chisomo cha Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu. Pakuti sitilemba kwa inu zina, koma zimene muwerenga, kapenanso muvomereza; ndipo ndiyembekeza kuti mudzavomereza kufikira chimaliziro; monganso munativomerezera ife pena, kuti ife ndife kudzitamandira kwanu, monga momwe inunso muli kudzitamandira kwathu m'tsiku la Ambuye wathu Yesu. Ndipo m'kulimbika kumene ndinafuna kudza kwa inu kale, kuti mukakhale nacho chisomo chachiwiri; ndipo popyola kwanu kupita ku Masedoniya, ndi kudzanso kwa inu pobwera kufuma ku Masedoniya; ndi kuperekezedwa ndi inu ku Yudeya. Pamenepo, pakufuna chimene, kodi ndinachitapo kosinthasintha? Kapena zimene nditsimikiza mtima kodi ndizitsimikiza mtima monga mwa thupi? Kuti pa ine pakhale eya, eya, ndi iai, iai? Koma Mulungu ali wokhulupirika, kuti mau athu a kwa inu sanakhala eya ndi iai. Pakuti Mwana wa Mulungu, Yesu Khristu, amene analalikidwa mwa inu ndi ife, (ine ndi Silivano ndi Timoteo) sanakhala eya ndi iai, koma anakhala eya mwa Iye. Pakuti monga mawerengedwe a malonjezano a Mulungu ali mwa Iye eya; chifukwa chakenso ali mwa Iye Amen, kwa ulemerero wa Mulungu mwa ife. Koma Iye wakutikhazika pamodzi ndi inu kwa Khristu, natidzoza ife, ndiye Mulungu; amenenso anatisindikiza chizindikiro, natipatsa chikole cha Mzimu mu mitima yathu. Koma ine ndiitana Mulungu akhale mboni pa moyo wanga, kuti kulekera inu ndinaleka kudza ku Korinto. Si kuti tichita ufumu pa chikhulupiriro chanu, koma tikhala othandizana nacho chimwemwe chanu; pakuti ndi chikhulupiriro muimadi. Koma ndinatsimikiza mtima mwa ine ndekha, ndisadzenso kwa inu ndi chisoni. Pakuti ngati ine ndimvetsa inu chisoni, ndaninso amene adzandikondweretsa ine, koma iye amene ndammvetsa chisoni? Ndipo ndinalemba ichi chomwe, kuti pakudza ndisakhale nacho chisoni kwa iwo amene ayenera kukondweretsa ine; ndi kukhulupirira mwa inu nonse, kuti chimwemwe changa ndi chanu cha inu nonse. Pakuti m'chisautso chambiri ndi kuwawa mtima ndinalembera inu ndi misozi yambiri; si kuti ndikumvetseni chisoni, koma kuti mukadziwe chikondi cha kwa inu, chimene ndili nacho koposa. Koma ngati wina wachititsa chisoni, sanachititsa chisoni ine, koma pena (kuti ndisasenzetse) inu nonse. Kwa wotereyo chilango ichi chidachitika ndi ambiri chikwanira; kotero kwina kuti inu mumkhululukire ndi kumtonthoza, kuti wotereyo akakamizidwe ndi chisoni chochulukacho. Chifukwa chake ndikupemphani inu kuti mumtsimikizire ameneyo chikondi chanu. Pakuti chifukwa cha ichi ndalembanso, kuti ndidziwe mayesedwe anu, ngati muli omvera m'zonse. Koma amene mumkhululukira kanthu, inenso nditero naye; pakuti chimene ndakhululukira inenso, ngati ndakhululukira kanthu, ndachichita chifukwa cha inu, pamaso pa Khristu; kuti asatichenjerere Satana; pakuti sitikhala osadziwa machenjerero ake. Koma pamene ndinadza ku Troasi kudzalalikira Uthenga Wabwino wa Khristu, ndipo pamene padanditsegukira kwa ine pakhomo, mwa Ambuye, ndinalibe mpumulo mu mzimu wanga, posapeza ine Tito mbale wanga; koma polawirana nao ndinanka ku Masedoniya. Koma ayamikike Mulungu, amene atitsogolera m'chigonjetso mwa Khristu, namveketsa fungo la chidziwitso chake mwa ife pamalo ponse. Pakuti ife ndife fungo labwino la Khristu, kwa Mulungu, mwa iwo akupulumutsidwa, ndi mwa iwo akuonongeka; kwa ena fungo la imfa kuimfa; koma kwa ena fungo la moyo kumoyo. Ndipo azikwanira ndani izi? Pakuti sitikhala monga ambiriwo, akuchita malonda nao mau a Mulungu; koma monga mwa choona mtima, koma monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tilankhula mwa Khristu. Kodi tilikuyambanso kudzivomereza tokha? Kapena kodi tisowa, monga ena, akalata otivomerezetsa kwa inu, kapena ochokera kwa inu? Inu ndinu kalata wathu, wolembedwa mu mitima yathu, wodziwika ndi wowerengedwa ndi anthu onse; popeza mwaonetsedwa kuti muli kalata wa Khristu, wakumtumikira ndi ife, wosalembedwa ndi kapezi iai, koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo; wosati m'magome amiyala, koma m'magome a mitima yathupi. Ndipo kulimbika kotere kwa Mulungu tili nako mwa Khristu: si kuti tili okwanira pa ife tokha, kuyesera kanthu monga mochokera mwa ife tokha; kukwanira kwathu kuchokera kwa Mulungu; amenenso anatikwaniritsa ife tikhale atumiki a pangano latsopano; si la chilembo, koma la mzimu; pakuti chilembo chipha, koma mzimu uchititsa moyo. Koma ngati utumiki wa imfa wolembedwa ndi wolochedwa m'miyala, unakhala m'ulemerero, kotero kuti ana a Israele sanathe kuyang'anitsa pa nkhope yake ya Mose, chifukwa cha ulemerero wa nkhope yake, umene unalikuchotsedwa: koposa kotani nanga utumiki wa Mzimu udzakhala m'ulemerero? Pakuti ngati utumiki wa chitsutso unali wa ulemerero, makamaka utumiki wa chilungamo uchulukira muulemerero kwambiri. Pakutinso chimene chinachitidwa cha ulemerero sichinachitidwa cha ulemerero m'menemo, chifukwa cha ulemerero woposawo. Pakuti ngati chimene chilikuchotsedwa chinakhala m'ulemerero, makamaka kwambiri chotsalacho chili m'ulemerero. Pokhala nacho tsono chiyembekezo chotere, tilankhula ndi kukhazikika mtima kwakukulu, ndipo si monga Mose, amene anaika chophimba pa nkhope yake, kuti ana a Israele asayang'anitse pa chimaliziro cha chimene chinalikuchotsedwa; koma mitima yao inaumitsidwa; pakuti kufikira lero lomwe lino, pa kuwerenga kwa pangano lakale chophimba chomwechi chikhalabe chosavundukuka, chimene chilikuchotsedwa mwa Khristu. Koma kufikira lero, pamene awerengedwa Mose, chophimba chigona pamtima pao. Koma pamene akatembenukira kwa Mulungu, chophimbacho chichotsedwa. Koma Ambuye ndiye Mzimuyo; ndipo pamene pali Mzimu wa Ambuye pali ufulu. Koma ife tonse ndi nkhope yosaphimbika popenyerera monga mwa kalirole ulemerero wa Ambuye, tisandulika m'chithunzithunzi chomwechi kuchokera kuulemerero kunka kuulemerero, monga ngati kuchokera kwa Ambuye Mzimu. Chifukwa chake popeza tili nao utumiki umene, monga talandira chifundo, sitifooka; koma takaniza zobisika za manyazi, osayendayenda mochenjerera, kapena kuchita nao mau a Mulungu konyenga; koma ndi maonekedwe a choonadi; tidzivomeretsa tokha ku chikumbu mtima cha anthu onse pamaso pa Mulungu. Koma ngatinso Uthenga Wabwino wathu uphimbika, uphimbika mwa iwo akutayika; mwa amene mulungu wa nthawi yino ya pansi pano unachititsa khungu maganizo ao a osakhulupirira, kuti chiwalitsiro cha Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Khristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawawalire. Pakuti tilalikira si za ife tokha, koma Yesu Khristu Ambuye, ndi ife tokha akapolo anu, chifukwa cha Khristu. Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kutuluka mumdima, ndiye amene anawala m'mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziwitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Khristu. Koma tili nacho chuma ichi m'zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife; ndife osautsika monsemo, koma osapsinjika; osinkhasinkha, koma osakhala kakasi; olondoleka, koma osatayika; ogwetsedwa, koma osaonongeka; nthawi zonse tilikusenzasenza m'thupi kufa kwake kwa Yesu, kuti moyonso wa Yesu uoneke m'thupi mwathu. Pakuti ife amene tili ndi moyo tiperekeka kuimfa nthawi zonse, chifukwa cha Yesu, kuti moyonso wa Yesu uoneke m'thupi lathu lakufa. Chotero imfa ichita mwa ife, koma moyo mwa inu. Koma pokhala nao mzimu womwewo wa chikhulupiriro, monga mwa cholembedwacho, ndinakhulupirira, chifukwa chake ndinalankhula; ifenso tikhulupirira, chifukwa chake tilankhula; podziwa kuti Iye amene anaukitsa Ambuye Yesu adzaukitsa ifenso pamodzi ndi Yesu, nadzatiikapo pamodzi ndi inu. Pakuti zonsezi nza kwa inu, kuti chisomocho, chochulukitsidwa mwa unyinjiwo, chichulukitsire chiyamiko ku ulemerero wa Mulungu. Chifukwa chake sitifooka; koma ungakhale umunthu wathu wakunja uvunda, wa m'kati mwathu ukonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku. Pakuti chisautso chathu chopepuka cha kanthawi chitichitira ife kulemera koposa kwakukulu ndi kosatha kwa ulemerero; popeza sitipenyerera zinthu zooneka, koma zinthu zosaoneka; pakuti zinthu zooneka zili za nthawi, koma zinthu zosaoneka zili zosatha. Pakuti tidziwa kuti ngati nyumba ya pansi pano ya msasa wathu ipasuka, tili nacho chimango cha kwa Mulungu, ndiyo nyumba yosamangidwa ndi manja, yosatha, m'Mwamba. Pakutinso m'menemo tibuula, ndi kukhumbitsa kuvekedwa ndi chokhalamo chathu chochokera Kumwamba; ngatitu povekedwa sitidzapezedwa amaliseche. Pakutinso ife okhala mu msasawu tibuula, pothodwa; si kunena kuti tifuna kuvulidwa, koma kuvekedwa, kuti chaimfacho chimezedwe ndi moyo. Ndipo wotikonzera ife ichi chimene, ndiye Mulungu, amene anatipatsa ife chikole cha Mzimu. Pokhala nako kulimbika mtima nthawi zonse tsono, ndipo podziwa kuti pamene tili kwathu m'thupi, sitili kwa Ambuye. (Pakuti tiyendayenda mwa chikhulupiriro si mwa chionekedwe); koma tilimbika mtima, ndipo tikondwera makamaka kusakhala m'thupi, ndi kukhala kwathu kwa Ambuye. Chifukwa chakenso tifunitsitsa, kapena kwathu kapena kwina, kukhala akumkondweretsa Iye. Pakuti ife tonse tiyenera kuonetsedwa kumpando wakuweruza wa Khristu, kuti yense alandire zochitika m'thupi, monga momwe anachita, kapena chabwino kapena choipa. Podziwa tsono kuopsa kwa Ambuye, tikopa anthu, koma tionetsedwa kwa Mulungu; ndipo ndiyembekezanso kuti tionetsedwa m'zikumbu mtima zanu. Sitidzivomeretsanso ife tokha kwa inu, koma tikupatsani inu chifukwa cha kudzitamandira pa ife, kuti mukakhale nako kanthu kakutsutsana nao iwo akudzitamandira pooneka pokha, osati mumtima. Pakuti ngati tili oyaluka, titero kwa Mulungu; ngati tili a nzeru zathu, titero kwa inu. Pakuti chikondi cha Khristu chitikakamiza; popeza taweruza chotero, kuti mmodzi adafera onse, chifukwa chake onse adafa; ndipo adafera onse kuti iwo akukhala ndi moyo asakhalenso ndi moyo kwa iwo okha, koma mwa Iye amene adawafera iwo, nauka. Kotero kuti ife sitidziwanso munthu tsopano monga mwa thupi; ndipo ngati tazindikira Khristu monga mwa thupi, koma tsopano sitimzindikiranso motero. Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano. Koma zinthu zonse zichokera kwa Mulungu amene anatiyanjanitsa kwa Iye yekha mwa Khristu, natipatsa utumiki wa chiyanjanitso; ndiko kunena kuti Mulungu anali mwa Khristu, alinkuyanjanitsa dziko lapansi kwa Iye yekha, osawawerengera zolakwa zao; ndipo anaikiza kwa ife mau a chiyanjanitso. Chifukwa chake tili atumiki m'malo mwa Khristu, monga ngati Mulungu alikudandaulira mwa ife; tiumiriza inu m'malo mwa Khristu, yanjanitsidwani ndi Mulungu. Ameneyo sanadziwa uchimo anamyesera uchimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye. Ndipo ochita naye pamodzi tidandauliranso kuti musalandire chisomo cha Mulungu kwachabe inu, (pakuti anena, M'nyengo yolandiridwa ndinamva iwe, ndipo m'tsiku la chipulumutso ndinakuthandiza. Taonani, tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa, taonani, tsopano ndilo tsiku la chipulumutso); osapatsa chokhumudwitsa konse m'chinthu chilichonse, kuti utumikiwo usanenezedwe; koma m'zonse tidzitsimikizira ife tokha monga atumiki a Mulungu, m'kupirira kwambiri, m'zisautso, m'zikakamizo, m'zopsinja, m'mikwingwirima, m'ndende, m'maphokoso, m'mavutitso, m'madikiro, m'masalo a chakudya; m'mayeredwe, m'chidziwitso, m'chilekerero, m'kukoma mtima, mwa Mzimu Woyera, m'chikondi chosanyenga; m'mau a choonadi, mu mphamvu ya Mulungu; mwa zida za chilungamo kulamanja ndi kulamanzere, mwa ulemerero, mwa mnyozo, mwa mbiri yoipa ndi mbiri yabwino; monga osocheretsa, angakhale ali oona; monga osadziwika, angakhale adziwika bwino; monga alinkufa, ndipo taonani tili ndi moyo; monga olangika, ndipo osaphedwa; monga akumva chisoni, koma akukondwera nthawi zonse; monga aumphawi, koma akulemeretsa ambiri; monga okhala opanda kanthu, ndipo akhala nazo zinthu zonse. M'kamwa mwathu mmotseguka kwa inu Akorinto, mtima wathu wakulitsidwa. Simupsinjika mwa ife, koma mupsinjika mumtima mwanu. Ndipo kukhale chibwezero chomwechi (ndinena monga ndi ana anga) mukulitsidwe inunso. Musakhale omangidwa m'goli ndi osakhulupirira osiyana; pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima? Ndipo Khristu avomerezana bwanji ndi Beliyali? Kapena wokhulupirira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupirira? Ndipo chiphatikizo chake nchanji ndi Kachisi wa Mulungu ndi wa mafano? Pakuti ife ndife Kachisi wa Mulungu wamoyo; monga Mulungu anati, Ndidzakhalitsa mwa iwo, ndipo ndidzayendayenda mwa iwo; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, ndi iwo adzakhala anthu anga. Chifukwa chake, Tulukani pakati pao, ndipo patukani, ati Ambuye, Ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka; ndipo Ine ndidzalandira inu, ndipo ndidzakhala kwa inu Atate, ndi inu mudzakhala kwa Ine ana aamuna ndi aakazi, anena Ambuye Wamphamvuyonse. Pokhala nao tsono malonjezano amenewa, okondedwa, tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m'kuopa Mulungu. Tipatseni malo; sitinamchitira munthu chosalungama, sitinaipsa munthu, sitinachenjerera munthu. Sindinena ichi kuti ndikutsutseni: pakuti ndanena kale kuti muli mu mitima yathu, kuti tife limodzi ndi kukhala ndi moyo limodzi. Ndilimbika mtima kwambiri pakunena nanu, kudzitamandira kwanga chifukwa cha inu nkwakukulu; ndidzazidwa nacho chitonthozo, ndisefukira nacho chimwemwe m'chisautso chathu chonse. Pakutinso pakudza ife Masedoniya thupi lathu linalibe mpumulo, koma tinasautsidwa ife monsemo; kunjako zolimbana, m'katimo mantha. Koma Iye amene atonthoza odzichepetsa, ndiye Mulungu, anatitonthoza ife ndi kufika kwake kwa Tito; koma si ndi kufika kwake kokha, komanso ndi chitonthozo chimene anatonthozedwa nacho mwa inu, pamene anatiuza ife kukhumbitsa kwanu, kulira kwanu, changu chanu cha kwa ine; kotero kuti ndinakondwera koposa. Kuti ngakhale ndakumvetsani chisoni ndi kalata uja, sindiwawapo mtima, ndingakhale ndinawawa mtima; pakuti ndiona kuti kalata uja anakumvetsani chisoni, ngakhale kwa nthawi yokha. Tsopano ndikondwera, si kuti mwangomvedwa chisoni, koma kuti mwamvetsedwa chisoni ku kutembenuka mtima; pakuti munamvetsedwa chisoni cha kwa Mulungu, kuti tisakusowetseni m'kanthu kalikonse. Pakuti chisoni cha kwa Mulungu titembenuzira mtima kuchipulumutso, chosamvetsanso chisoni; koma chisoni cha dziko lapansi chichita imfa. Pakuti, taonani, ichi chomwe, chakuti mudamvetsedwa chisoni cha kwa Mulungu, khama lalikulu lanji chidalichita mwa inu, komanso chodzikonza, komanso mkwiyo, komanso mantha, komanso kukhumbitsa komanso changu, komanso kubwezera chilango! M'zonse munadzitsimikizira nokha kuti muli oyera mtima m'menemo. Chifukwa chake ndingakhale ndalembera kwa inu, sindinachita chifukwa cha iye amene anachita choipa, kapena chifukwa cha iye amene anachitidwa choipa, koma kuti khama lanu la kwa ife lionetsedwe kwa inu pamaso pa Mulungu. Chifukwa cha ichi tatonthozedwa; ndipo m'chitonthozo chathu tinakondwera koposa ndithu pa chimwemwe cha Tito, kuti mzimu wake unatsitsimutsidwa ndi inu nonse. Pakuti ngati ndadzitamandira nako kanthu kwa iye chifukwa cha inu, sindinamvetsedwa manyazi; koma monga tinalankhula zonse ndi inu m'choonadi, koteronso kudzitamandira kwathu kumene kwa Tito, kunakhala choonadi. Ndipo chikondi chenicheni chake chichulukira koposa kwa inu, pokumbukira kumvera kwanu kwa inu nonse, kuti munamlandira iye ndi mantha ndi kunthunthumira. Ndikondwera kuti m'zonse ndilimbika mtima za inu. Ndipo tikudziwitsani, abale, chisomo cha Mulungu chopatsika mwa Mipingo ya ku Masedoniya, kuti m'chitsimikizo chachikulu cha chisautso, kuchulukitsa kwa chimwemwe chao, ndi kusauka kwao, kwenikweni zidachulukira ku cholemera cha kuolowa mtima kwao. Pakuti monga mwa mphamvu yao, ndichitapo umboni, inde koposa mphamvu yao, anachita eni ake, natiumiriza ndi kutidandaulira za chisomocho, ndi za chiyanjano cha utumiki wa kwa oyera mtima; ndipo, si monga tidayembekeza; koma anayamba kudzipereka okha kwa Ambuye, ndi kwa ife mwa chifuniro cha Mulungu. Kotero kuti tinadandaulira Tito, kuti monga anayamba kale, chomwechonso atsirize kwa inu chisomo ichinso. Koma monga muchulukira m'zonse, m'chikhulupiriro, ndi m'mau, ndi m'chidziwitso, ndi m'khama lonse, ndi m'chikondi chanu cha kwa ife, chulukaninso m'chisomo ichi. Sindinena ichi monga kulamulira, koma kuyesa mwa khama la ena choonadi cha chikondi chanunso. Pakuti mudziwa chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti, chifukwa cha inu anakhala wosauka, angakhale anali wolemera, kuti inu ndi kusauka kwake mukakhale olemera. Ndipo m'menemo nditchula choyesa ine; pakuti chimene chipindulira inu, amene munayamba kale chaka chapitachi si kuchita kokha, komanso kufunira. Koma tsopano tsirizani kuchitaku; kuti monga kunali chivomerezo cha kufunira, koteronso kukhale kutsiriza kwake m'chimene muli nacho. Pakuti ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chimsowa. Pakuti sinditero kuti ena akamasuke, ndi inu musautsidwe; koma mwa kulingana kuchuluka kwanu kukwanire kusowa kwao nthawi ya makono ano, kutinso kuchuluka kwao kukwanire kusowa kwanu. Kuti pakhale chilingano; monga kwalembedwa, Wosonkhetsa chambiri sichinamtsalira; ndi iye wosonkhetsa pang'ono sichinamsowa. Koma ayamikike Mulungu, wakupatsa khama lomweli la kwa inu mu mtima wa Tito. Pakutitu analandira kudandaulira kwathu; koma pokhala nalo khama loposa, anatulukira kunka kwa inu mwini wake. Ndipo tatuma pamodzi naye mbaleyo, amene kusimba kwake m'Uthenga Wabwino kuli m'Mipingo yonse; ndipo si ichi chokha, komanso anasankhika ndi Mipingo, apite limodzi ndi ife m'chisomo ichi, chimene tichitumikira ife, kwa ulemerero wa Ambuye, ndi kuonetsa chivomerezo chathu; ndi kupewa ichi kuti wina angatitchule za kuchulukira kumene tikutumikira; pakuti tikonzeratu zinthu zokoma, si pamaso pa Ambuye pokha, komanso pamaso pa anthu. Ndipo tinatumiza mbale wathu awaperekeze iwo, amene tamtsimikizira kawirikawiri ali wakhama m'zinthu zambiri, koma tsopano wa khama loposatu ndi kulimbika kwakukulu kumene ali nako kwa inu. Nanga za Tito, ali woyanjana wanga ndi wochita nane wa kwa inu; nanga abale athu, ali atumwi a Mipingo, ali ulemerero wa Khristu. Chifukwa chake muwatsimikizire iwo chitsimikizo cha chikondi chanu, ndi cha kudzitamandira kwathu pa inu pamaso pa Mipingo. Pakutitu za utumiki wa kwa oyera mtima sikufunika kwa ine kulembera inu; pakuti ndidziwa chivomerezo chanu chimene ndidzitamandira nacho chifukwa cha inu ndi Amasedoniya, kuti Akaya anakonzekeratu chitapita chaka; ndi changu chanu chinautsa ochulukawo. Koma ndatuma abale kuti kudzitamandira kwathu kwa pa inu kusakhale kopanda pake m'menemo; kuti, monga ndinanena, mukakhale okonzekeratu; kuti kapena akandiperekeze a ku Masedoniya nadzakupezani inu osakonzeka, ife (kuti tisanene inu) tingachititsidwe manyazi m'kulimbika kumene. Chifukwa chake ndinayesa kuti kufunika kupempha abale kuti atsogole afike kwa inu, nakonzeretu dalitso lanu lolonjezeka kale, kuti chikhale chokonzeka chomwechi, monga ngati mdalitso, ndipo si monga mwa kuumiriza. Koma nditi ichi, kuti iye wakufesa mouma manja, mouma manjanso adzatuta. Ndipo iye wakufesa moolowa manja, moolowa manjanso adzatuta. Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera. Ndipo Mulungu akhoza kuchulukitsira chisomo chonse kwa inu; kuti inu, pokhala nacho chikwaniro chonse m'zinthu zonse, nthawi zonse, mukachulukire kuntchito yonse yabwino; monga kwalembedwa, Anabalalitsa, anapatsa kwa osauka; chilungamo chake chikhale kunthawi yonse. Ndipo iye wopatsa mbeu kwa wofesa, ndi mkate ukhale chakudya, adzapatsa ndi kuchulukitsa mbeu yanu yofesa, nadzaonjezapo pa zipatso za chilungamo chanu; polemeretsedwa inu m'zonse kukuolowa manja konse, kumene kuchita mwa ife chiyamiko cha kwa Mulungu. Pakuti utumiki wa kutumikira kumene sudzaza zosowa za oyera mtima zokha, koma uchulukiranso kwa Mulungu mwa mayamiko ambiri; popeza kuti mwa kuyesa kwa utumiki umene alemekeza Mulungu pa kugonja kwa chivomerezo chanu ku Uthenga Wabwino wa Khristu, ndi kwa kuolowa manja kwa chigawano chanu kwa iwo ndi kwa onse; ndipo iwo, ndi pempherero lao la kwa inu, akhumbitsa inu, chifukwa cha chisomo choposa cha Mulungu pa inu. Ayamikike Mulungu chifukwa cha mphatso yakeyake yosatheka kuneneka. Koma ine ndekha Paulo, ndidandaulira inu mwa kufatsa ndi ulere wa Khristu, ine amene pamaso panu ndikhala wodzichepetsa pakati pa inu, koma pokhala kwina ine ndilimbika mtima kwa inu; koma ndipempha kuti pokhala ndili pomwepo, ndisalimbike mtima ndi kulimbika kumene ndiyesa kulimbika nako pa ena, amene atiyesera ife monga ngati tilikuyendayenda monga mwa thupi. Pakuti pakuyendayenda m'thupi, sitichita nkhondo monga mwa thupi, (pakuti zida za nkhondo yathu sizili za thupi, koma zamphamvu mwa Mulungu zakupasula malinga); ndi kugwetsa matsutsano, ndi chokwezeka chonse chimene chidzikweza pokana chidziwitso cha Mulungu, ndi kugonjetsa ganizo lonse kukumvera kwa Khristu; ndi kukhala okonzeka kubwezera chilango kusamvera konse, pamene kumvera kwanu kudzakwaniridwa. Kodi mupenyera zopenyeka pamaso? Ngati wina alimbika mwa yekha kuti ali wa Khristu, ayesere ichinso mwa iye yekha, kuti monga iye ali wa Khristu, koteronso ife. Pakuti ndingakhale ndikadzitamandira kanthu kochulukira za ulamuliro (umene anatipatsa Ambuye kukumangirira, ndipo si kukugwetsera kwanu), sindidzanyazitsidwa; kuti ndisaoneke monga ngati kukuopsani mwa akalatawo. Pakuti, akalatatu, ati, ndiwo olemera, ndi amphamvu; koma maonekedwe a thupi lake ngofooka, ndi mau ake ngachabe. Woteroyo ayese ichi kuti monga tili ife ndi mau mwa akalata, pokhala palibe ife, tili oterenso m'machitidwe pokhala tili pomwepo. Pakuti sitilimba mtima kudziwerenga, kapena kudzilinganiza tokha ndi ena a iwo amene adzivomeretsa okha; koma iwowa, podziyesera okha ndi iwo okha, ndi kudzilinganiza okha ndi iwo okha, alibe nzeru. Koma ife sitidzadzitamandira popitirira muyeso, koma monga mwa muyeso wa chilekezero chimene Mulungu anatigawira muyeso, kufikira ngakhale kwa inunso. Pakuti sitinyanyampiradi tokha, monga ngati sitinafikira kwa inu; pakuti tinadza kufikira inunso, mu Uthenga Wabwino wa Khristu: osadzitamandira popitirira muyeso mwa machititso a ena; koma tili nacho chiyembekezo kuti pakukula chikhulupiriro chanu, tidzakulitsidwa mwa inu monga mwa chilekezero chathu kwa kuchulukira, kukalalikira Uthenga Wabwino m'tsogolo mwake mwa inu, sikudzitamandira mwa chilekezero cha wina, ndi zinthu zokonzeka kale. Koma iye wodzitamandira adzitamandire mwa Ambuye; pakuti si iye amene adzitama yekha, koma iye amene Ambuye amtama ali wovomerezeka. Bwenzi mutandilola pang'ono ndi chopusacho! Komanso mundilole. Pakuti ndichita nsanje pa inu ndi nsanje ya Mulungu; pakuti ndinakupalitsani ubwenzi mwamuna mmodzi, kuti ndikalangize inu ngati namwali woyera mtima kwa Khristu. Koma ndiopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Heva ndi kuchenjerera kwake, maganizo anu angaipsidwe kusiyana nako kuona mtima ndi kuyera mtima zili kwa Khristu. Pakutitu ngati iye wakudza alalikira Yesu wina, amene ife sitinalalikira, kapena ngati mulandira mzimu wa mtundu wina, umene simunalandira, kapena Uthenga Wabwino wa mtundu wina umene simunalandira, mulolana naye bwino lomwe. Pakuti ndiyesa kuti sindinaperewera konse ndi atumwi oposatu. Ndipo ndingakhale ndili wosaphunzira m'manenedwe, koma sinditero m'chidziwitso, koma m'zonse tachionetsa kwa inu mwa anthu onse. Kodi ndachimwa podzichepetsa ndekha, kuti inu mukakwezedwe, popeza ndinalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu mwaufulu? Ndinalanda za Mipingo ina, ndi kulandira kwa iwo kulipira kuti ndikatumikire inu; ndipo pakukhala nanu, ndi kusowa, sindinasaukitsa munthu aliyense; pakuti abale akuchokera ku Masedoniya, anakwaniritsa kusowa kwanga; ndipo m'zonse ndinachenjera ndekha, ndisalemetse inu, ndipo ndidzachenjerapo. Choonadi cha Khristu chili mwa ine, kuti kudzitamandira kumene sikudzaletsedwa kwa ine mu mbali za Akaya. Chifukwa ninji? Chifukwa sindikonda inu kodi? Adziwa Mulungu. Koma chimene ndichita, ndidzachitanso, kuti ndikawadulire chifukwa iwo akufuna chifukwa; kuti m'mene adzitamandiramo, apezedwe monganso ife. Pakuti otere ali atumwi onyenga, ochita ochenjerera, odzionetsa ngati atumwi a Khristu. Ndipo kulibe kudabwa; pakuti Satana yemwe adzionetsa ngati mngelo wa kuunika. Chifukwa chake sikuli kanthu kwakukulu ngatinso atumiki ake adzionetsa monga atumiki a chilungamo; amene chimaliziro chao chidzakhala monga ntchito zao. Ndinenanso, Munthu asandiyese wopanda nzeru; koma ngati mutero, mundilandirenso ine monga wopanda nzeru, kuti inenso ndidzitamandire pang'ono. Chimene ndilankhula sindilankhula monga mwa Ambuye, koma monga wopanda nzeru, m'kulimbika kumene kwa kudzitamandira. Popeza ambiri adzitamandira monga mwa thupi, inenso ndidzadzitamandira. Pakuti mulolana nao opanda nzeru mokondwera, pokhala anzeru inu nokha. Pakuti mulola ngati wina akuyesani inu akapolo, ngati wina alikwira inu, ngati wina alanda zanu, ngati wina adzikuza, ngati wina akupandani pankhope. Ndinena monga mwa kunyoza, monga ngati tinakhala ofooka. Koma m'mene wina alimbika mtimamo (ndinena mopanda nzeru) momwemo ndilimbika mtima inenso. Kodi ali Ahebri? Inenso. Kodi ali Aisraele? Inenso. Kodi ali mbeu ya Abrahamu? Inenso. Kodi ali atumiki a Khristu? (Ndilankhula monga moyaluka), makamaka ine; m'zivutinso mochulukira, m'ndende mochulukira, m'mikwingwirima mosawerengeka, muimfa kawirikawiri. Kwa Ayuda ndinalandira kasanu mikwingwirima makumi anai kuperewera umodzi. Katatu ndinamenyedwa ndi ndodo, kamodzi ndinaponyedwa miyala, katatu ndinatayika posweka chombo, ndinakhala m'kuya tsiku limodzi usana ndi usiku; paulendo kawirikawiri, moopsa mwake mwa mitsinje, moopsa mwake mwa olanda, moopsa modzera kwa mtundu wanga, moopsa modzera kwa amitundu, moopsa m'mudzi, moopsa m'chipululu, moopsa m'nyanja, moopsa mwa abale onyenga; m'chivutitso ndi m'cholemetsa, m'madikiro kawirikawiri, m'njala ndi ludzu, m'masalo a chakudya kawirikawiri, m'chisanu ndi umaliseche. Popanda zakunjazo pali chondisindikiza tsiku ndi tsiku, chalabadiro cha Mipingo yonse. Afooka ndani wosafooka inenso? Akhumudwitsidwa ndani, wosatenthanso ine? Ngati ndiyenera kudzitamandira, ndidzadzitamandira ndi za kufooka kwanga. Mulungu Atate wa Ambuye Yesu, Iye amene alemekezeka kunthawi yonse, adziwa kuti sindinama. M'Damasiko kazembe wa mfumu Areta analindizitsa mudzi wa Adamasiko kuti andigwire ine; ndipo mwa zenera, mudengu, ananditsitsa pakhoma, ndipo ndinapulumuka m'manja mwake. Ndiyenera kudzitamandira, kungakhale sikupindulika; koma ndidzadza kumasomphenya ndi mavumbulutso a Ambuye. Ndidziwa munthu wa mwa Khristu, zitapita zaka khumi ndi zinai (ngati m'thupi, sindidziwa; ngati kunja kwa thupi, sindidziwa; adziwa Mulungu), anakwatulidwa wotereyo kunka naye Kumwamba kwachitatu. Ndipo ndidziwa munthu wotereyo (ngati m'thupi, ngati wopanda thupi, sindidziwa; adziwa Mulungu), kuti anakwatulidwa kunka ku Paradaiso, namva maneno osatheka kuneneka, amene saloleka kwa munthu kulankhula. Chifukwa cha wotereyo ndidzadzitamandira; koma chifukwa cha ine ndekha sindidzadzitamandira, koma m'zofooka zanga. Pakuti ngati ndikafuna kudzitamandira, sindidzakhala wopanda nzeru; pakuti ndidzanena choonadi; koma ndileka, kuti wina angandiwerengere ine koposa kumene andiona ine, kapena amva za ine. Ndipo kuti ndingakwezeke koposa, chifukwa cha ukulu woposa wa mavumbulutso, kunapatsidwa kwa ine munga m'thupi, ndiye mngelo wa Satana kuti anditundudze, kuti ndingakwezeke koposa. Za ichi ndinapemphera Ambuye katatu kuti chichoke kwa ine. Ndipo ananena kwa ine, Chisomo changa chikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa m'ufooko. Chifukwa chake makamaka ndidzadzitamandira mokondweratu m'mafooko anga, kuti mphamvu ya Khristu ikhale pa ine. Chifukwa chake ndisangalala m'mafooko, m'ziwawa, m'zikakamizo, m'mazunzo, m'zipsinjiko, chifukwa cha Khristu; pakuti pamene ndifooka, pamenepo ndili wamphamvu. Ndakhala wopanda nzeru, mwandichititsa kutero; pakuti inu munayenera kundivomereza; pakuti sindiperewera ndi atumwi oposatu m'kanthu konse, ndingakhale ndili chabe. Zizindikirotu za mtumwi zinachitika pakati pa inu, m'chipiriro chonse, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi zamphamvu. Pakuti kuli chiyani chimene munachepetsedwa nacho ndi Mipingo yotsala ina, ngati si ichi kuti ine ndekha sindinasaukitsa inu? Ndikhululukireni choipa ichi. Taonani, nthawi yachitatu iyi ndapukwa ine kudza kwa inu, ndipo sindidzakusaukitsani; pakuti sindifuna zanu, koma inu; pakuti ana sayenera kuunjikira atate ndi amai, koma atate ndi amai kuunjikira ana. Ndipo ndidzapereka ndi kuperekedwa konse chifukwa cha miyoyo yanu mokondweratu. Ngati ndikonda inu kochuluka koposa, kodi ndikondedwa kochepa? Koma kukhale kotero; ine sindinalemetsa inu; koma pokhala wochenjera ine, ndinakugwirani ndi chinyengo. Kodi wina wa iwo ndinawatuma kwa inu, ndinakuchenjererani naye kodi? Ndinadandaulira Tito, ndipo ndinatuma mbaleyo naye. Kodi Tito anakuchenjererani kanthu? Sitinayendayenda naye Mzimu yemweyo kodi? Sitinatsata mapazi omwewo kodi? Mumayesa tsopano lino kuti tilikuwiringula kwa inu. Tilankhula pamaso pa Mulungu mwa Khristu. Koma zonse, okondedwa, zili za kumangirira kwanu. Pakuti ndiopa, kuti kaya, pakudza ine, sindidzakupezani inu otere onga ndifuna, ndipo ine ndidzapezedwa ndi inu wotere wonga simufuna; kuti kaya pangakhale chotetana, kaduka, mikwiyo, zilekanitso, maugogodi, ukazitape, zodzikuza, mapokoso; kuti pakudzanso ine, Mulungu wanga angandichepse pa inu, ndipo ndingalirire ambiri a iwo amene adachimwa kale, osalapa pa chodetsa, ndi chigololo, ndi kukhumba zonyansa zimene anachita. Nthawi yachitatu iyi ndilinkudza kwa inu. Pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu maneno onse adzakhazikika. Ndinanena kale, ndipo ndinena ndisanafikeko, monga pamene ndinali pomwepo kachiwiri kaja, pokhala ine palibe, kwa iwo adachimwa kale ndi kwa onse otsala, kuti, ngati ndidzanso sindidzawaleka; popeza mufuna chitsimikizo, cha Khristu wakulankhula mwa ine; amene safooka kwa inu, koma ali wamphamvu mwa inu; pakuti anapachikidwa m'ufooko, koma ali ndi moyo mu mphamvu ya Mulungu. Pakuti ifenso tili ofooka mwa Iye, koma tidzakhala ndi moyo pamodzi ndi Iye, mu mphamvu ya Mulungu, ya kwa inu. Dziyeseni nokha, ngati muli m'chikhulupiriro, dzitsimikizeni nokha. Kapena simuzindikira kodi za inu nokha kuti Yesu Khristu ali mwa inu? Mukapanda kukhala osatsimikizidwa. Koma ndiyembekeza kuti mudzazindikira kuti sitili osatsimikizidwa. Ndipo tipemphera Mulungu kuti musachite kanthu koipa; sikuti ife tikaoneke ovomerezeka, koma kuti inu mukachite chabwino, tingakhale ife tikhala monga osatsimikizidwa. Pakuti sitikhoza kanthu pokana choonadi, koma povomereza choonadi. Pakuti tikondwera, pamene ife tifooka ndi inu muli amphamvu; ichinso tipempherera, ndicho ungwiro wanu. Chifukwa cha ichi ndilembera izi pokhala palibe ine, kuti pokhala ndili pomwepo ndingachite mowawitsa, monga mwa ulamuliro umene Ambuye anandipatsa ine wakumangirira, ndipo si wakugwetsa. Chotsalira, abale, kondwerani. Muchitidwe angwiro; mutonthozedwe; khalani a mtima umodzi, khalani mumtendere; ndipo Mulungu wa chikondi ndi mtendere akhale pamodzi ndi inu. Mupatsane moni ndi chipsompsono chopatulika. Oyera mtima onse akupatsani moni. Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu, ndi chikondi cha Mulungu, ndi chiyanjano cha Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse. Paulo, mtumwi (wosachokera kwa anthu, kapena mwa munthu, koma mwa Yesu Khristu, ndi Mulungu Atate, amene anamuukitsa Iye kwa akufa), ndi abale onse amene ali pamodzi ndi ine, kwa Mipingo ya ku Galatiya: Chisomo kwa inu, ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anadzipereka yekha chifukwa cha machimo athu, kuti akatilanditse ife m'nyengo ya pansi pano yino yoipa, monga mwa chifuniro cha Mulungu ndi Atate wathu; yemweyo akhale nao ulemerero kunthawi za nthawi. Amen. Ndizizwa kuti msanga motere mulikupatuka kwa iye amene anakuitanani m'chisomo cha Khristu, kutsata Uthenga Wabwino wina; umene suli wina; koma pali ena akuvuta inu, nafuna kuipsa Uthenga Wabwino wa Khristu. Koma ngakhale ife, kapena mngelo wochokera Kumwamba, ngati akakulalikireni Uthenga Wabwino wosati umene tidakulalikirani ife, akhale wotembereredwa. Monga tinanena kale, ndipo ndinenanso tsopano apa, ngati wina akulalikirani Uthenga Wabwino wosati umene mudaulandira, akhale wotembereredwa. Pakuti kodi ndikopa anthu tsopano, kapena Mulungu? Kapena kodi ndifuna kukondweretsa anthu? Ndikadakhala wokondweretsabe anthu, sindikadakhala kapolo wa Khristu. Pakuti ndikudziwitsani inu, abale, za Uthenga Wabwinowo wolalikidwa ndi ine, kuti suli monga mwa anthu. Pakutitu sindinaulandira kwa munthu, kapena sindinauphunzira, komatu unadza mwa vumbulutso la Yesu Khristu. Pakuti mudamva za makhalidwe anga kale mwa Chiyuda, kuti ndinalondalonda Mpingo wa Mulungu koposa, ndi kuupasula, ndipo ndinawaposa ndi kutsogola mwa Chiyuda ambiri a msinkhu wanga mwa mtundu wanga, ndipo ndinakhala wachangu koposa pa miyambo ya makolo anga. Koma pamene padakondweretsa Mulungu, amene anandipatula, ndisanabadwe, nandiitana ine mwa chisomo chake, kuti avumbulutse Mwana wake mwa ine, kuti ndimlalikire Iye mwa amitundu; pomwepo sindinafunsana ndi thupi ndi mwazi: kapena kukwera kunka ku Yerusalemu sindinankako kwa iwo amene anakhala atumwi ndisanakhale mtumwi ine, komatu ndinamuka ku Arabiya, ndipo ndinabweranso ku Damasiko. Pamenepo patapita zaka zitatu, ndinakwera kunka ku Yerusalemu kukazindikirana naye Kefa, ndipo ndinakhala kwa iye masiku khumi ndi asanu. Koma wina wa atumwi sindinamuona, koma Yakobo mbale wa Ambuye. Ndipo izi ndikulemberani inu, taonani, pamaso pa Mulungu sindinama ine. Pamene ndinadza kumbali za Siriya ndi Silisiya. Koma ndinali wosadziwika nkhope yanga kwa Mipingo ya ku Yudeya ya mwa Khristu; koma analinkumva kokha, kuti, Iye wakutilondalonda ife kale, tsopano alalikira chikhulupirirocho adachipasula kale; ndipo analemekeza Mulungu mwa ine. Pamenepo popita zaka khumi ndi zinai ndinakweranso kunka ku Yerusalemu pamodzi ndi Barnabasi, ndinamtenganso Tito andiperekeze. Koma ndinakwera kunkako movumbulutsa; ndipo ndinawauza Uthenga Wabwino umene ndiulalikira kwa amitundu; koma m'tseri kwa iwo omveka, kuti kapena ndingathamange, kapena ndikadathamanga chabe. Komatu ngakhale Tito, amene anali ndi ine, ndiye Mgriki, sanamkakamiza adulidwe; ndicho chifukwa cha abale onyenga olowezedwa m'tseri, amene analowa m'tseri kudzazonda ufulu wathu umene tili nao mwa Khristu Yesu, kuti akatichititse ukapolo. Koma sitidawafumukira mowagonjera ngakhale ora limodzi; kuti choonadi cha Uthenga Wabwino chikhalebe ndi inu. Koma iwo akuyesedwa ali kanthu (ngati anali otani kale, kulibe kanthu kwa ine; Mulungu salandira nkhope ya munthu) iwo omvekawo sanandionjezera ine kanthu; koma pena, pakuona kuti anaikiza kwa ine Uthenga Wabwino wa kusadulidwa, monga kwa Petro Uthenga Wabwino wa mdulidwe (pakuti Iye wakuchita mwa Petro kumtuma kwa odulidwa anachitanso mwa ine kundituma kwa amitundu); ndipo pakuzindikira chisomocho chinapatsidwa kwa ine, Yakobo ndi Kefa ndi Yohane, amene anayesedwa mizati, anapatsa ine ndi Barnabasi dzanja lamanja la chiyanjano, kuti ife tipite kwa amitundu, ndi iwo kwa mdulidwe; pokhapo kuti tikumbukire aumphawi; ndicho chomwe ndinafulumira kuchichita. Koma pamene Kefa anadza ku Antiokeya ndinatsutsana naye pamaso pake, pakuti anatsutsika wolakwa. Pakuti asanafike ena ochokera kwa Yakobo, anadya pamodzi ndi amitundu; koma atadza iwo, anadzibweza, ndi kudzipatula yekha, pakuopa iwo a ku mdulidwe. Ndipo Ayuda otsala anawagwiranso m'maso pamodzi naye; kotero kuti Barnabasinso anatengedwa ndi kugwira m'maso kwao. Komatu pamene ndinaona kuti sanalikuyenda koongoka, monga mwa choonadi cha Uthenga Wabwino, ndinati kwa Kefa pamaso pa onse, Ngati inu muli Myuda mutsata makhalidwe a amitundu, ndipo si a Ayuda, mukakamiza bwanji amitundu atsate makhalidwe a Ayuda? Ife ndife Ayuda pachibadwidwe, ndipo sitili ochimwa a kwa amitundu; koma podziwa kuti munthu sayesedwa wolungama pa ntchito ya lamulo, koma mwa chikhulupiriro cha Yesu Khristu, ifedi tinakhulupirira kwa Khristu Yesu, kuti tikayesedwe olungama ndi chikhulupiriro cha Khristu, ndipo si ndi ntchito za lamulo; pakuti palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi ntchito za lamulo. Koma ngati ife, pofuna kuyesedwa olungama mwa Khristu, tipezedwanso tili ochimwa tokha, kodi Khristu ali mtumiki wa uchimo chifukwa chake? Msatero ai. Pakuti ngati izi zomwezi ndazigumula ndidzimanganso, ndidzitsimikizira ndekha ndili wolakwa. Pakuti ine mwa lamulo ndafa kulamulo, kuti ndikhale ndi moyo kwa Mulungu. Ndinapachikidwa ndi Khristu; koma ndili ndi moyo; wosatinso ine ai, koma Khristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndili nao tsopano m'thupi, ndili nao m'chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine. Sindichiyesa chopanda pake chisomo cha Mulungu; pakuti ngati chilungamo chili mwa lamulo, Khristu adafa chabe. Agalatiya opusa inu, anakulodzani ndani, inu amene Yesu Khristu anaonetsedwa pa maso panu, wopachikidwa? Ichi chokha ndifuna kuphunzira kwa inu, Kodi munalandira Mzimuyo ndi ntchito za lamulo, kapena ndi kumva kwa chikhulupiriro? Kodi muli opusa otere? Popeza mudayamba ndi Mzimu, kodi tsopano mutsiriza ndi thupi? Kodi mudamva zowawa zambiri zotere kwachabe? Ngatitu kwachabe. Ndipo iye amene akuonjezerani inu Mzimuyo, nachita zimphamvu mwa inu, atero kodi ndi ntchito za lamulo, kapena ndi kumva kwa chikhulupiriro? Monga Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kunawerengedwa kwa iye chilungamo, chotero zindikirani kuti iwo a chikhulupiriro ndiwo ana a Abrahamu. Ndipo malembo, pakuoneratu kuti Mulungu adzayesa olungama amitundu ndi chikhulupiriro, anayamba kale kulalikira Uthenga Wabwino kwa Abrahamu, kuti, Idzadalitsidwa mwa iwe mitundu yonse. Kotero kuti iwo a chikhulupiriro adalitsidwa pamodzi ndi Abrahamu wokhulupirikayo. Pakuti onse amene atama ntchito za lamulo liwakhalira temberero; pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa aliyense wosakhala m'zonse zolembedwa m'buku la chilamulo, kuzichita izi. Ndipo chidziwikatu kuti palibe munthu ayesedwa wolungama ndi lamulo pamaso pa Mulungu; pakuti, Wolungama adzakhala ndi moyo ndi chikhulupiriro; koma chilamulo sichichokera kuchikhulupiriro; koma, Wakuzichita izi adzakhala ndi moyo ndi izi. Khristu anatiombola ku temberero la chilamulo, atakhala temberero m'malo mwathu; pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa aliyense wopachikidwa pamtengo. Kuti dalitso la Abrahamu mwa Khristu Yesu, lichitike kwa amitundu; kuti tikalandire lonjezano la Mzimuyo, mwa chikhulupiriro. Abale, ndinena monga munthu. Pangano, lingakhale la munthu, litalunzika, palibe munthu aliyesa chabe, kapena kuonjezapo. Ndipo malonjezano ananenedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake. Sanena, Ndipo kwa zimbeu, ngati kunena zambiri; komatu ngati kunena imodzi, Ndipo kwa mbeu yako, ndiye Khristu. Ndipo ichi ndinena: Lamulo, limene linafika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi atatu, silifafaniza pangano lolunzika kale ndi Mulungu, kuliyesa lonjezanolo lachabe. Pakuti ngati kulowa nyumba kuchokera kulamulo, sikuchokeranso kulonjezano; koma kumeneku Mulungu anampatsa Abrahamu kwaufulu mwa lonjezano. Nanga chilamulo tsono? Chinaonjezeka chifukwa cha zolakwa, kufikira ikadza mbeu imene adailonjezera; ndipo chinakonzeka ndi angelo m'dzanja la nkhoswe. Koma nkhoswe siili ya mmodzi; koma Mulungu ali mmodzi. Pamenepo kodi chilamulo chitsutsana nao malonjezano a Mulungu? Msatero ai. Pakuti chikadapatsidwa chilamulo chakukhoza kuchitira moyo, chilungamo chikadachokera ndithu kulamulo. Komatu lembo linatsekereza zonse pansi pa uchimo, kuti lonjezano la kwa chikhulupiriro cha Yesu Khristu likapatsidwe kwa okhulupirirawo. Koma chisanadze chikhulupiriro tinasungidwa pomvera lamulo otsekedwa kufikira chikhulupiriro chimene chikavumbulutsidwa bwinobwino. Momwemo chilamulo chidakhala namkungwi wathu wakutifikitsa kwa Khristu, kuti tikayesedwe olungama ndi chikhulupiriro. Koma popeza chadza chikhulupiriro, sitikhalanso omvera namkungwi. Pakuti inu nonse muli ana a Mulungu, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu. Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Khristu mudavala Khristu. Muno mulibe Myuda, kapena Mgriki, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; pakuti muli nonse mmodzi mwa Khristu Yesu. Koma ngati muli a Khristu, muli mbeu ya Abrahamu, nyumba monga mwa lonjezano. Koma ndinena kuti, pokhala wolowa nyumba ali wakhanda, sasiyana ndi kapolo, angakhale ali mwini zonse; komatu ali wakumvera omsungira ndi adindo, kufikira nthawi yoikika kale ndi atate wake. Koteronso ife, pamene tinali akhanda, tinali akapolo akumvera miyambo ya dziko lapansi; koma pokwaniridwa nthawi, Mulungu anatuma Mwana wake, wobadwa ndi mkazi, wobadwa wakumvera lamulo, kuti akaombole iwo akumvera lamulo, kuti ife tikalandire umwana. Ndipo popeza muli ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wake alowe m'mitima yathu, wofuula Abba! Atate! Kotero kuti sulinso kapolo, koma mwana; koma ngati mwana, wolowa nyumbanso mwa Mulungu. Komatu pajapo, posadziwa Mulungu inu, munachitira ukapolo iyo yosakhala milungu m'chibadwidwe chao; koma tsopano, podziwa Mulungu inu, koma makamaka podziwika ndi Mulungu, mubwereranso bwanji kutsata miyambo yofooka ndi yaumphawi, imene mufuna kubwerezanso kuichitira ukapolo? Musunga masiku, ndi miyezi, ndi nyengo, ndi zaka. Ndiopera inu, kuti kapena ndadzivutitsa ndi inu chabe. Abale, ndikupemphani, khalani monga ine, pakuti inenso ndili monga inu. Simunandichitira choipa ine; koma mudziwa kuti m'kufooka kwa thupi ndinakulalikirani Uthenga Wabwino poyamba: ndipo chija cha m'thupi langa chakukuyesani inu simunachipeputsa, kapena sichinakunyansirani, komatu munandilandira ine monga mngelo wa Mulungu, monga Khristu Yesu mwini. Pamenepo thamo lanu lili kuti? Pakuti ndikuchitirani inu umboni, kuti, kukadatheka, mukadakolowola maso anu ndi kundipatsa ine. Kotero kodi ndasanduka mdani wanu, pakukunenerani zoona? Achita changu pa inu koma si kokoma ai, komatu afuna kukutsekerezani inu kunja, kuti mukawachitire iwowa changu. Koma nkwabwino kuchita changu m'zabwino nthawi zonse, si pokhapokha pokhala nanu pamodzi ine. Tiana tanga, amene ndilikumvanso zowawa za kubala inu, kufikira Khristu aumbika mwa inu, koma mwenzi nditakhala nanu tsopano, ndi kusintha mau anga; chifukwa ndisinkhasinkha nanu. Ndiuzeni, inu akufuna kukhala omvera lamulo, kodi simukumva chilamulo? Pakuti palembedwa, kuti Abrahamu anali nao ana amuna awiri, mmodzi wobadwa mwa mdzakazi, ndi mmodzi wobadwa mwa mfulu. Komatu uyo wa mdzakazi anabadwa monga mwa thupi; koma iye wa mfuluyo, anabadwa monga mwa lonjezano. Izo ndizo zophiphiritsa; pakuti akaziwa ali mapangano awiri, mmodzi wa kuphiri la Sinai, akubalira ukapolo, ndiye Hagara. Koma Hagara ndiye phiri la Sinai, m'Arabiya, nafanana ndi Yerusalemu wa tsopano; pakuti ali muukapolo pamodzi ndi ana ake. Koma Yerusalemu wa kumwamba uli waufulu, ndiwo amai wathu. Pakuti kwalembedwa, Kondwera, chumba iwe wosabala; imba nthungululu, nufuule iwe wosamva kuwawa kwa kubala; pakuti ana ake a iye ali mbeta achuluka koposa ana a iye ali naye mwamuna. Koma ife, abale, monga Isaki, tili ana a lonjezano. Komatu monga pompaja iye wobadwa monga mwa thupi anazunza wobadwa monga mwa Mzimu, momwemonso tsopano. Koma lembo linena chiyani? Taya kubwalo mdzakazi ndi mwana wake, pakuti sadzalowa nyumba mwana wa mdzakazi pamodzi ndi mwana wa mfulu. Chifukwa chake, abale, sitili ana a mdzakazi, komatu a mfulu. Khristu anatisandutsa mfulu, kuti tikhale mfulu; chifukwa chake chilimikani, musakodwenso ndi goli la ukapolo. Taonani, ine Paulo ndinena ndi inu, kuti, ngati mulola akuduleni, Khristu simudzapindula naye kanthu. Ndichitanso umboni kwa munthu yense wolola amdule, kuti ali wamangawa kuchita chilamulo chonse. Mulibe kanthu ndi Khristu, inu amene muyesedwa olungama ndi lamulo; mudagwa posiyana nacho chisomo. Pakuti ife mwa Mzimu, kuchokera m'chikhulupiriro, tilindira chiyembekezo cha chilungamo. Pakuti mwa Khristu Yesu kapena mdulidwe kapena kusadulidwa kulibe mphamvu; komatu chikhulupiriro, chakuchititsa mwa chikondi. Munathamanga bwino; anakuletsani ndani kuti musamvere choonadi? Kukopa kumene sikuchokera kwa Iye anakuitanani. Chotupitsa pang'ono chitupitsa mtanda wonse. Ine ndikhulupirira inu mwa Ambuye, kuti simudzakhala nao mtima wina; koma iye wakuvuta inu, angakhale ali yani, adzasenza chitsutso chake. Koma ine, abale, ngati ndilalikiranso mdulidwe, ndizunzikanso bwanji? Pamenepo chikhumudwitso cha mtanda chidatha. Mwenzi atadzidula, iwo akugwedezetsani inu. Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nao ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwachikondi chitiranani ukapolo. Pakuti mau amodzi akwaniritsa chilamulo chonse ndiwo; Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini. Koma ngati mulumana ndi kudyana, chenjerani mungaonongane. Koma ndinena, Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse chilakolako cha thupi. Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna musazichite. Ngati Mzimu akutsogolerani, simuli omvera lamulo. Ndipo ntchito za thupi zionekera, ndizo dama, chodetsa, kukhumba zonyansa, kupembedza mafano, nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko, njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo, monga ndachita, kuti iwo akuchitachita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu. Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo. Koma iwo a Khristu Yesu adapachika thupi, ndi zokhumba zake, ndi zilakolako zake. Ngati tili ndi moyo ndi Mzimu, ndi Mzimunso tiyende. Tisakhale odzikuza, outsana, akuchitirana njiru. Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso. Nyamuliranani zothodwetsa, ndipo kotero mufitse chilamulo cha Khristu. Pakuti ngati wina ayesa ali kanthu pokhala ali chabe, adzinyenga yekha. Koma yense ayesere ntchito yake ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha, si chifukwa cha wina. Pakuti yense adzasenza katundu wake wa iye mwini. Koma iye amene aphunzira mau, ayenera kuchereza womphunzitsayo m'zonse zabwino. Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta. Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m'thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa Mzimu, chochokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha. Koma tisaleme pakuchita zabwino; pakuti pa nyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka. Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro. Taonani, malembedwe akuluwo ndakulemberani inu ndi dzanja langa la ine mwini. Onse amene afuna kuonekera okoma m'thupi, iwowa akukakamizani inu mudulidwe; chokhacho, chakuti angazunzike chifukwa cha mtanda wa Khristu. Pakuti angakhale iwo omwe odulidwa sasunga lamulo; komatu afuna inu mudulidwe, kuti akadzitamandire m'thupi lanu. Koma kudzitamandira ine konsekonse, iai, koma mu mtanda wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene mwa Iye dziko lapansi lapachikidwira ine, ndi ine ndapachikidwira dziko lapansi. Pakuti mdulidwe ulibe kanthu, kusadulidwa kulibe kanthunso, komatu wolengedwa watsopano. Ndipo onse amene atsatsa chilangizo ichi, mtendere ndi chifundo zikhale pa iwo, ndi pa Israele wa Mulungu. Kuyambira tsopano palibe munthu andivute, pakuti ndili nayo ine m'thupi mwanga mikwingwirima ya Yesu. Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wanu, abale. Amen. Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu, mwa chifuniro cha Mulungu, kwa oyera mtima amene ali m'Efeso, ndi kwa iwo okhulupirika mwa Khristu Yesu: Chisomo kwa inu, ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu. Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Khristu; monga anatisankha ife mwa Iye, lisanakhazikike dziko lapansi, tikhale ife oyera mtima, ndi opanda chilema pamaso pake m'chikondi. Anatikonzeratu tilandiridwe ngati ana a Iye yekha mwa Yesu Khristu, monga umo kunakomera chifuniro chake, kuti uyamikidwe ulemerero wa chisomo chake, chimene anatichitira ife kwaufulu mwa Wokondedwayo. Tili ndi maomboledwe mwa mwazi wake, chikhululukiro cha zochimwa, monga mwa kulemera kwa chisomo chake, chimene anatichulukitsira ife m'nzeru zonse, ndi chisamaliro. Anatizindikiritsa ife chinsinsi cha chifuniro chake, monga kunamkomera ndi monga anatsimikiza mtima kale mwa Iye, kuti pa makonzedwe a makwaniridwe a nyengozo, akasonkhanitse pamodzi zonse mwa Khristu, za kumwamba, ndi za padziko. Mwa Iye tinayesedwa cholowa chake, popeza tinakonzekeratu monga mwa chitsimikizo mtima cha Iye wakuchita zonse monga mwa uphungu wa chifuniro chake; kuti ife amene tinakhulupirira Khristu kale tikayamikitse ulemerero wake. Mwa Iyeyo inunso, mutamva mau a choonadi, Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu, ndi kumkhulupirira Iye, munasindikizidwa chizindikiro ndi Mzimu Woyera wa lonjezano, ndiye chikole cha cholowa chathu, kuti akeake akaomboledwe, ndi kuti ulemerero wake uyamikike. Mwa ichi inenso, m'mene ndamva za chikhulupiriro cha mwa Ambuye Yesu chili mwa inu ndi chikondi chanu, chimenenso mufikitsira oyera mtima onse, sindileka kuyamika chifukwa cha inu, ndi kukumbukira inu m'mapemphero anga; kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa ulemerero, akupatseni inu mzimu wa nzeru, ndi wa vumbulutso kuti mukamzindikire Iye; ndiko kunena kuti maso a mitima yanu awalitsike, kuti mukadziwe inu chiyembekezo cha kuitana kwake nchiyani; chiyaninso chuma cha ulemerero wa cholowa chake mwa oyera mtima, ndi chiyani ukulu woposa wa mphamvu yake ya kwa ife okhulupirira, monga mwa machitidwe a mphamvu yake yolimba, imene anachititsa mwa Khristu, m'mene anamuukitsa kwa akufa, namkhazikitsa pa dzanja lake lamanja m'zakumwamba, pamwamba pa ukulu wonse, ndi ulamuliro, ndi mphamvu, ndi ufumu, ndi dzina lililonse lotchedwa, si m'nyengo yino ya pansi pano yokha, komanso mwa iyo ikudza; ndipo anakonza zonse pansi pa mapazi ake, nampatsa Iye akhale mutu pamtu pa zonse, kwa Mpingo amene ali thupi lake, mdzazidwe wa Iye amene adzaza zonse m'zonse. Ndipo inu, anakupatsani moyo, pokhala munali akufa ndi zolakwa, ndi zochimwa zanu, zimene munayendamo kale, monga mwa mayendedwe a dziko lapansi lino, monga mwa mkulu wa ulamuliro wa mlengalenga, wa mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera; amene ife tonsenso tinagonera pakati pao kale, m'zilakolako za thupi lathu, ndi kuchita zifuniro za thupi, ndi za maganizo, ndipo tinali ana a mkwiyo chibadwire, monganso otsalawo; koma Mulungu, wolemera chifundo, chifukwa cha chikondi chake chachikulu chimene anatikonda nacho, tingakhale tinali akufa m'zolakwa zathu, anatipatsa moyo pamodzi ndi Khristu (muli opulumutsidwa ndi chisomo), ndipo anatiukitsa pamodzi, natikhazikitsa pamodzi m'zakumwamba mwa Khristu Yesu; kuti akaonetsere m'nthawi zilinkudza chuma choposa cha chisomo chake, m'kukoma mtima kwa pa ife mwa Khristu Yesu. Pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiriro, ndipo ichi chosachokera kwa inu: chili mphatso ya Mulungu; chosachokera kuntchito, kuti asadzitamandire munthu aliyense. Pakuti ife ndife chipango chake, olengedwa mwa Khristu Yesu, kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo. Momwemo kumbukirani, kuti kale inu amitundu m'thupi, otchedwa kusadulidwa ndi iwo otchedwa mdulidwe m'thupi, umene udachitika ndi manja; kuti nthawi ija munali opanda Khristu, alendo a padera ndi mbumba ya Israele, ndi alendo alibe kanthu ndi mapangano a malonjezano, opanda chiyembekezo, ndi opanda Mulungu m'dziko lapansi. Koma tsopano mwa Khristu Yesu inu amene munali kutali kale, anakusendezani mukhale pafupi m'mwazi wa Khristu. Pakuti Iye ndiye mtendere wathu, amene anachita kuti onse awiri akhale mmodzi, nagumula khoma lakudulitsa pakati, atachotsa udani m'thupi lake, ndiwo mau a chilamulo cha kutchulako malangizo; kuti alenge awiriwa mwa Iye yekha, akhale munthu mmodzi watsopano, ndi kuchitapo mtendere; ndi kuti akayanjanitse awiriwa ndi Mulungu, m'thupi limodzi mwa mtandawo, atapha nao udaniwo; ndipo m'mene anadza, analalikira Uthenga Wabwino wa mtendere kwa inu akutali, ndi mtendere kwa iwo apafupi; kuti mwa Iye ife tonse awiri tili nao malowedwe athu kwa Atate, mwa Mzimu mmodzi. Pamenepo ndipo simulinso alendo ndi ogonera, komatu muli a mudzi womwewo wa oyera mtima ndi a banja la Mulungu; omangika pa maziko a atumwi ndi aneneri, pali Khristu Yesu mwini, mwala wa pangodya; mwa Iye chimango chonse cholumikizika pamodzi bwino, chikula, chikhale Kachisi wopatulika mwa Ambuye; chimene inunso mumangidwamo pamodzi, mukhale chokhalamo Mulungu mwa Mzimu. Chifukwa cha ichi ine Paulo, ndine wandende wa Khristu Yesu chifukwa cha inu amitundu, ngatitu munamva za udindo wa chisomo cha Mulungu chimene anandipatsa ine cha kwa inu; ndi umo anandizindikiritsa chinsinsicho mwa vumbulutso, monga ndinalemba kale mwachidule, chimene mukhoza kuzindikira nacho, pakuchiwerenga, chidziwitso changa m'chinsinsi cha Khristu, chimene sanachizindikiritsa ana a anthu m'mibadwo ina, monga anachivumbulutsa tsopano kwa atumwi ndi aneneri ake oyera mwa Mzimu, kuti amitundu ali olowa nyumba pamodzi ndi ife, ndi ziwalo zinzathu za thupilo, ndi olandira nafe pamodzi palonjezano mwa Khristu Yesu, mwa Uthenga Wabwino, umene anandikhalitsa mtumiki wake monga mwa mphatso ya chisomo cha Mulungu, chimene anandipatsa ine, monga mwa machitidwe a mphamvu yake. Kwa ine wochepa ndi wochepetsa wa onse oyera mtima anandipatsa chisomo ichi ndilalikire kwa amitundu chuma chosalondoleka cha Khristu; ndi kuwalitsira onse adziwe makonzedwe a chinsinsicho, chimene chinabisika kuyambira kalekale mwa Mulungu wolenga zonse; kuti mu Mpingo azindikiritse tsopano kwa akulu ndi maulamuliro m'zakumwamba nzeru ya mitundumitundu ya Mulungu, monga mwa chitsimikizo mtima cha nthawi za nthawi, chimene anachita mwa Khristu Yesu Ambuye wathu: amene tili naye chokhazikika mtima ndi chiyandiko cholimbika, mwa chikhulupiriro cha pa Iye. Mwa ichi ndipempha kuti musade mtima m'zisautso zanga chifukwa cha inu, ndiwo ulemerero wanu. Chifukwa cha ichi ndipinda maondo anga kwa Atate, amene kuchokera kwa Iye fuko lonse la m'mwamba ndi la padziko alitcha dzina, kuti monga mwa chuma cha ulemerero wake akulimbikitseni inu ndi mphamvu mwa Mzimu wake, m'kati mwanu, kuti Khristu akhale chikhalire mwa chikhulupiriro m'mitima yanu; kuti, ozika mizu ndi otsendereka m'chikondi, mukakhozetu kuzindikira pamodzi ndi oyera mtima onse, kupingasa, ndi utali, ndi kukwera, ndi kuzama nchiyani; ndi kuzindikira chikondi cha Khristu, chakuposa mazindikiridwe, kuti mukadzazidwe kufikira chidzalo chonse cha Mulungu. Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife, kwa Iye ukhale ulemerero mu Mpingo ndi mwa Khristu Yesu, kufikira mibadwo yonse ya nthawi za nthawi. Amen. Ndikudandaulirani inu tsono, ine wandende mwa Ambuye, muyende koyenera maitanidwe amene munaitanidwa nao, ndi kuonetsera kudzichepetsa konse, ndi chifatso, ndi kuonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzake, mwa chikondi; ndi kusamalitsa kusunga umodzi wa Mzimu mwa chimangiriro cha mtendere. Thupi limodzi ndi Mzimu mmodzi, monganso anakuitanani m'chiyembekezo chimodzi cha maitanidwe anu; Ambuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi, Mulungu mmodzi ndi Atate wa onse amene ali pamwamba pa onse, ndi mwa onse, ndi m'kati mwa zonse. Ndipo kwa yense wa ife chapatsika chisomo, monga mwa muyeso wa mphatso ya Khristu. Chifukwa chake anena, M'mene anakwera kumwamba, anamanga ndende undende, naninkha zaufulu kwa anthu. Koma ichi, chakuti, Anakwera, nchiyani nanga koma kuti anatsikiranso ku madera a kunsi kwa dziko? Iye wotsikayo ndiye yemweyonso anakwera, popitiriratu miyamba yonse, kuti akadzaze zinthu zonse. Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi; kuti akonzere oyera mtima kuntchito ya utumiki, kumangirira thupi la Khristu; kufikira ife tonse tikafikira ku umodzi wa chikhulupiriro, ndi wa chizindikiritso cha Mwana wa Mulungu, kwa munthu wangwiro, ku muyeso wa msinkhu wa chidzalo cha Khristu. Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa; koma ndi kuchita zoona mwa chikondi tikakule m'zinthu zonse, kufikira Iye amene ali mutu ndiye Khristu; kuchokera mwa Iye thupi lonse, lolukidwa ndi lolumikizidwa pamodzi, pothandizanapo mfundo yonse, monga mwa kuchititsa kwa chiwalo chonse pa muyeso wake, lichita makulidwe a thupi, kufikira chimango chake mwa chikondi. Pamenepo ndinena ichi, ndipo ndichita umboni mwa Ambuye, kuti simuyendanso inu monganso amitundu angoyenda, m'chitsiru cha mtima wao, odetsedwa m'nzeru zao, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu, chifukwa cha chipulukiro chili mwa iwo, chifukwa cha kuumitsa kwa mitima yao; amenewo popeza sazindikiranso kanthu konse, anadzipereka okha kuti akhumbe zonyansa, kuti achite chidetso chonse mu umbombo. Koma inu simunaphunzira Khristu chotero, ngatitu mudamva Iye, ndipo munaphunzitsidwa mwa Iye, monga choonadi chili mwa Yesu; kuti muvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, wovunda potsata zilakolako za chinyengo; koma kuti mukonzeke, mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu, nimuvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m'chilungamo, ndi m'chiyero cha choonadi. Mwa ichi, mutataya zonama, lankhulani zoona yense ndi mnzake; pakuti tili ziwalo wina ndi mnzake. Kwiyani, koma musachimwe; dzuwa lisalowe muli chikwiyire, ndiponso musampatse malo mdierekezi. Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake, kuti akhale nacho chakuchereza wosowa. Nkhani yonse yovunda isatuluke m'kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva. Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu, amene munasindikizidwa chizindikiro mwa Iye, kufikira tsiku la maomboledwe. Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse. Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Khristu anakhululukira inu. Chifukwa chake khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa; ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino. Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima; kapena chinyanso, ndi kulankhula zopanda pake, kapena zopusa zimene siziyenera; koma makamaka chiyamiko. Pakuti ichi muchidziwe kuti wadama yense, kapena wachidetso, kapena wosirira, amene apembedza mafano, alibe cholowa m'ufumu wa Khristu ndi Mulungu. Asakunyengeni inu munthu ndi mau opanda pake, pakuti chifukwa cha izi umadza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera. Chifukwa chake musakhale olandirana nao; pakuti kale munali mdima, koma tsopano muli kuunika mwa Ambuye; yendani monga ana a kuunika, pakuti chipatso cha kuunika tichipeza m'ubwino wonse, ndi chilungamo, ndi choonadi, kuyesera chokondweretsa Ambuye nchiyani; ndipo musayanjane nazo ntchito za mdima zosabala kanthu, koma makamakanso muzitsutse; pakuti zochitidwa nao m'tseri, kungakhale kuzinena kuchititsa manyazi. Koma zinthu zonse potsutsika ndi kuunika, zionekera; pakuti chonse chakuonetsa chili kuunika. Mwa ichi anena, Khala maso wogona iwe, nuuke kwa akufa, ndipo Khristu adzawala pa iwe. Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi, popeza masiku ali oipa. Chifukwa chake musakhale opusa, koma dziwitsani chifuniro cha Ambuye nchiyani. Ndipo musaledzere naye vinyo, m'mene muli chitayiko; komatu mudzale naye Mzimu, ndi kudzilankhulira nokha ndi masalmo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuimbira ndi kuimba m'malimba Ambuye mumtima mwanu; ndi kuyamika Mulungu Atate masiku onse, chifukwa cha zonse, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu; ndi kumverana wina ndi mnzake m'kuopa Khristu. Akazi inu, mverani amuna anu a inu eni, monga kumvera Ambuye. Pakuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Khristu ndiye mutu wa Mpingo, ali yekha Mpulumutsi wa thupilo. Komatu monga Mpingo amvera Khristu, koteronso akazi amvere amuna ao m'zinthu zonse. Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Khristu anakonda Mpingo, nadzipereka yekha m'malo mwake; kuti akampatule, atamyeretsa ndi kumsambitsa madzi ndi mau; kuti Iye akadziikire yekha Mpingo wa ulemerero, wopanda banga, kapena khwinya, kapena kanthu kotere; komatu kuti akhale woyera, ndi wopanda chilema. Koteronso amuna azikonda akazi ao a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha. Wokonda mkazi wa iye yekha, adzikonda yekha; pakuti munthu sanadana nalo thupi lake ndi kale lonse; komatu alilera nalisunga, monganso Khristu Mpingo; pakuti tili ziwalo za thupi lake. Chifukwa cha ichi munthu azisiya atate ndi amai, nadzaphatikizana ndi mkazi wake; ndipo iwo awiri adzakhala thupi limodzi. Chinsinsi ichi nchachikulu; koma ndinena ine za Khristu ndi Mpingo. Komanso inu, yense pa yekha, yense akonde mkazi wake wa iye yekha, monga adzikonda yekha; ndipo mkaziyo akumbukire kuti aziopa mwamuna. Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi nchabwino. Lemekeza atate wako ndi amai ako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano), kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthawi yaikulu padziko. Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m'maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye. Akapolo inu, mverani iwo amene ali ambuye anu monga mwa thupi, ndi kuwaopa ndi kunthunthumira nao, ndi mtima wanu wosakumbukira kanthu kena, monga kwa Khristu; si monga mwa ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu monga akapolo a Khristu, akuchita chifuniro cha Mulungu chochokera kumtima; akuchita ukapolo ndi kuvomereza mtima, monga kutumikira Ambuye Yesu Khristu, si anthu ai; podziwa kuti chinthu chokoma chilichonse yense achichita, adzambwezera chomwechi Ambuye, angakhale ali kapolo kapena mfulu. Ndipo, ambuye, inu, muwachitire zomwezo iwowa, nimuleke kuwaopsa; podziwa kuti Ambuye wao ndi wanu ali m'Mwamba, ndipo palibe tsankho kwa Iye. Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yake. Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi. Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba. Mwa ichi mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima chitsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutachita zonse, mudzachilimika. Chifukwa chake chilimikani, mutadzimangira m'chuuno mwanu ndi choonadi, mutavalanso chapachifuwa cha chilungamo; ndipo mutadziveka mapazi anu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere; koposa zonse mutadzitengeranso chikopa cha chikhulupiriro, chimene mudzakhoza kuzima nacho mivi yonse yoyaka moto ya woipayo. Mutengenso chisoti cha chipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, ndilo Mau a Mulungu; mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse, ndi ine ndemwe, kuti andipatse mau m'kunditsegulira m'kamwa molimbika, kuti ndizindikiritse anthu chinsinsicho cha Uthenga Wabwino, chifukwa cha umene ndili mtumiki wa m'unyolo, kuti m'menemo ndikalankhule molimbika, monga ndiyenera kulankhula. Koma kuti mukadziwe inunso za kwa ine, zimene ndichita, zinthu zonse adzakuzindikiritsani Tikiko mbale wokondedwayo, ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye; amene ndamtuma kwa inu chifukwa cha ichicho, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti akatonthoze mitima yanu. Mtendere ukhale kwa abale, ndi chikondi, pamodzi ndi chikhulupiriro, zochokera kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye Yesu Khristu. Akhale nacho chisomo onse akukonda Ambuye wathu Yesu Khristu m'chosaonongeka. Paulo ndi Timoteo, akapolo a Yesu Khristu, kwa oyera mtima onse mwa Khristu Yesu, akukhala ku Filipi, pamodzi ndi oyang'anira ndi atumiki: Chisomo kwa inu ndi mtendere za kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu. Ndiyamika Mulungu wanga pokumbukira inu ponse; nthawi zonse m'pembedzero langa lonse la kwa inu nonse ndichita pembedzerolo ndi kukondwera, chifukwa cha chiyanjano chanu chakuthandizira Uthenga Wabwino, kuyambira tsiku loyambalo, kufikira tsopano lino; pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu; monga kundiyenera ine kuyesa za inu nonse, popeza ndili nako m'mtima mwanga, kuti inu m'zomangira zanga, ndipo m'chodzikanira, ndi matsimikizidwe a Uthenga Wabwino, inu nonse muli oyanjana nane m'chisomo. Pakuti Mulungu ali mboni yanga, kuti ndilakalaka inu nonse m'phamphu la mwa Khristu Yesu. Ndipo ichi ndipempha, kuti chikondi chanu chisefukire chionjezere, m'chidziwitso, ndi kuzindikira konse; kuti mukayese inu zinthu zosiyana; kuti mukakhale a mtima woona ndi wosalakwa, kufikira tsiku la Khristu; odzala nacho chipatso cha chilungamo, chimene chili mwa Yesu Khristu, kuchitira Mulungu ulemerero ndi chiyamiko. Koma abale, ndifuna kuti muzindikire kuti zija za kwa ine zidachita makamaka kuthandizira Uthenga Wabwino; kotero kuti zomangira zanga zinaonekera mwa Khristu m'bwalo lonse la alonda, ndi kwa onse ena; ndi kuti unyinji wa abale mwa Ambuye, pokhulupirira m'zomangira zanga, alimbika mtima koposa kulankhula mau a Mulungu opanda mantha. Enatu alalikiranso Khristu chifukwa cha kaduka ndi ndeu; koma enanso chifukwa cha kukoma mtima; ena atero ndi chikondi, podziwa kuti anandiika ndichite chokanira cha Uthenga Wabwino; koma ena alalikira Khristu mochokera m'chotetana, kosati koona, akuyesa kuti adzandibukitsira chisautso m'zomangira zanga. Potero nchiyani? Chokhacho kuti monsemo, ngati pamaso pokha, ngati m'choonadi, Khristu alalikidwa; ndipo m'menemo ndikondwera, komanso ndidzakondwera. Pakuti ndidziwa kuti ichi chidzandichitira ine chipulumutso, mwa pembedzero lanu ndi mwa kundipatsako kwa Mzimu wa Yesu Khristu; monga mwa kulingiriritsa ndi chiyembekezo changa, kuti palibe chinthu chidzandichititsa manyazi, komatu mwa kulimbika mtima konse, monga nthawi yonse, tsopanonso Khristu adzakuzidwa m'thupi langa, kapena mwa moyo, kapena mwa imfa. Pakuti kwa ine kukhala ndi moyo ndiko Khristu, ndi kufa kuli kupindula. Koma ngati kukhala ndi moyo m'thupi ndiko chipatso cha ntchito yanga, sindizindikiranso chimene ndidzasankha. Koma ndipanidwa nazo ziwirizi, pokhala nacho cholakalaka cha kuchoka kukhala ndi Khristu, ndiko kwabwino koposaposatu; koma kukhalabe m'thupi ndiko kufunika koposa, chifukwa cha inu. Ndipo pokhulupirira pamenepo ndidziwa kuti ndidzakhala, ndi kukhalitsa ndi inu nonse, kuonjezera chimwemwe cha chikhulupiriro chanu; kuti kudzitamandira kwanu kuchuluke m'Khristu Yesu mwa ine, mwa kukhalanso ine kwa inu. Chokhachi, mayendedwe anu ayenere Uthenga Wabwino wa Khristu: kuti, ndingakhale nditi ndilinkudza ndi kuona inu, ndingakhale nditi ndili kwina, ndikamva za kwa inu, kuti muchilimika mu mzimu umodzi, ndi kugwirira pamodzi ndi moyo umodzi chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino; osaopa adani m'kanthu konse, chimene chili kwa iwowa chisonyezo cha chionongeko, koma kwa inu cha chipulumutso, ndicho cha kwa Mulungu; kuti kwapatsidwa kwa inu kwaufulu chifukwa cha Khristu, si kukhulupirira kwa Iye kokha, komatunso kumva zowawa chifukwa cha Iye, ndi kukhala nacho inu chilimbano chomwechi mudachiona mwa ine, nimukumva tsopano chili mwa ine. Ngati tsono muli chitonthozo mwa Khristu, ngati chikhazikitso cha chikondi, ngati chiyanjano cha Mzimu, ngati phamphu, ndi zisoni, kwaniritsani chimwemwe changa, kuti mukalingalire mtima zomwezo, akukhala nacho chikondi chomwe, a moyo umodzi, olingalira mtima umodzi; musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini; munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake. Mukhale nao mtima m'kati mwanu umene unalinso mwa Khristu Yesu, ameneyo, pokhala nao maonekedwe a Mulungu, sanachiyesa cholanda kukhala wofana ndi Mulungu, koma anadzikhuthula yekha, natenga maonekedwe a kapolo, nakhala m'mafanizidwe a anthu; ndipo popezedwa m'maonekedwe ngati munthu, anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda. Mwa ichinso Mulungu anamkwezetsa Iye, nampatsa dzina limene liposa maina onse, kuti m'dzina la Yesu bondo lililonse lipinde, la za m'mwamba ndi za padziko, ndi za pansi pa dziko, ndi malilime onse avomere kuti Yesu Khristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate. Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokhapokha pokhala ine ndilipo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira; pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye Mulungu. Chitani zonse kopanda madandaulo ndi makani, kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chilema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m'dziko lapansi, akuonetsera mau a moyo; kuti ine ndikakhale wakudzitamandira nao m'tsiku la Khristu, kuti sindinathamanga chabe, kapena kugwiritsa ntchito chabe. Komatu ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira kwa chikhulupiriro chanu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse; momwemonso kondwerani inu, nimukondwere pamodzi ndi ine. Koma ndiyembekeza mwa Ambuye Yesu kuti ndidzatumiza Timoteo kwa inu msanga, kuti inenso nditonthozeke bwino pozindikira za kwa inu. Pakuti ndilibe wina wa mtima womwewo, amene adzasamalira za kwa inu ndi mtima woona. Pakuti onsewa atsata za iwo okha, si za Yesu Khristu. Koma muzindikira matsimikizidwe ake, kuti, monga mwana achitira atate wake, anatumikira pamodzi ndi ine Uthenga Wabwino. Ameneyo ndithu tsono ndiyembekeza kumtuma posachedwa m'mene ndikapenyerera za kwa ine zidzatani; koma ndikhulupirira mwa Ambuye kuti ine ndekhanso ndidzadza msanga. Koma ndinayesa nkufunika kutuma kwa inu Epafrodito mbaleyo, ndiye wantchito mnzanga ndi msilikali mnzanga, ndiye mtumwi wanu, ndi wonditumikira pa chosowa changa; popeza anali wolakalaka inu nonse, navutika mtima chifukwa mudamva kuti anadwala. Pakutinso anadwaladi pafupi imfa; komatu Mulungu anamchitira chifundo; koma si iye yekha, komatu inenso, kuti ndisakhale nacho chisoni chionjezereonjezere. Chifukwa chake ndamtuma iye chifulumizire, kuti pakumuona mukakondwerenso, ndi inenso chindichepere chisoni. Chifukwa chake mumlandire mwa Ambuye, ndi chimwemwe chonse; nimuchitire ulemu oterewa; pakuti chifukwa cha ntchito ya Khristu anafikira pafupi imfa, wosasamalira moyo wake, kuti akakwaniritse chiperewero cha utumiki wanu wa kwa ine. Chotsalira, abale anga, kondwerani mwa Ambuye. Kulembera zomwezo kwa inu, sikundivuta ine, koma kwa inu kuli kukhazikitsa. Penyererani agalu, penyererani ochita zoipa, penyererani choduladula; pakuti ife ndife mdulidwe, akutumikira popembedza ndi Mzimu wa Mulungu, nadzitamandira mwa Khristu Yesu, osakhulupirira m'thupi; ndingakhale inenso ndili nako kakukhulupirira m'thupi; ngati wina yense ayesa kukhulupirira m'thupi, makamaka ineyu; wodulidwa tsiku lachisanu ndi chitatu, wa mbadwo wa Israele, wa fuko la Benjamini, Muhebri wa mwa Ahebri; monga mwa lamulo, Mfarisi; monga mwa changu, wolondalonda Mpingo; monga mwa chilungamo cha m'lamulo wokhala wosalakwa ine. Komatu zonse zimene zinandipindulira, zomwezo ndinaziyesa chitayiko chifukwa cha Khristu. Komatu zenizeninso ndiyesa zonse zikhale chitayiko chifukwa cha mapambanidwe a chizindikiritso cha Khristu Yesu Ambuye wanga, chifukwa cha Iyeyu ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadzionjezere Khristu, ndi kupezedwa mwa Iye, wosati wakukhala nacho chilungamo changa cha m'lamulo, koma chimene cha mwa chikhulupiriro cha Khristu, chilungamocho chochokera mwa Mulungu ndi chikhulupiriro; kuti ndimzindikire Iye, ndi mphamvu ya kuuka kwake, ndi chiyanjano cha zowawa zake, pofanizidwa ndi imfa yake; ngati nkotheka ndikafikire kuuka kwa akufa. Si kunena kuti ndinalandira kale, kapena kuti ndatha kukonzeka wamphumphu; koma ndilondetsa, ngatinso ndikachigwire ichi chimene anandigwirira Khristu Yesu. Abale, ine sindiwerengera ndekha kuti ndatha kuchigwira: koma chinthu chimodzi ndichichita; poiwaladi zam'mbuyo, ndi kutambalitsira zam'tsogolo, ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Khristu Yesu. Tonsefe amene tsono tidakonzeka amphumphu, tilingirire ichi mumtima; ndipo ngati kuli kanthu mulingirira nako kwina mumtima, akanso Mulungu adzavumbulutsira inu; chokhachi, kumene tidafikirako, mayendedwe athu alinganeko. Abale, khalani pamodzi akutsanza anga, ndipo yang'anirani iwo akuyenda kotero monga muli ndi ife chitsanzo chanu. Pakuti ambiri amayenda, za amene ndinakuuzani kawirikawiri, ndipo tsopanonso ndikuuzani ndi kulira, ali adani a mtanda wa Khristu; chitsiriziro chao ndicho kuonongeka, mulungu wao ndiyo mimba yao, ulemerero wao uli m'manyazi ao, amene alingirira za padziko. Pakuti ufulu wathu uli Kumwamba; kuchokera komwenso tilindirira Mpulumutsi, Ambuye Yesu Khristu; amene adzasanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lake la ulemerero, monga mwa machitidwe amene akhoza kudzigonjetsera nao zinthu zonse. Potero, abale anga okondedwa, olakalakidwa, ndinu chimwemwe changa ndi korona wanga, chilimikani motere mwa Ambuye, okondedwa. Ndidandaulira Yuwodiya, ndidandaulira Sintike, alingirire ndi mtima umodzi mwa Ambuye. Inde, ndikupemphaninso, mnzanga wa m'goli woona, muthandize akazi awa amene anakangalika nane pamodzi mu Uthenga Wabwino, pamodzi ndi Klemensinso, ndi otsala aja antchito anzanga, amene maina ao ali m'buku la Moyo. Kondwerani mwa Ambuye nthawi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani. Kufatsa kwanu kuzindikirike ndi anthu onse. Ambuye ali pafupi. Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu. Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi. Zimenenso mudaziphunzira, ndi kuzilandira, ndi kuzimva, ndi kuziona mwa ine, zomwezo chitani; ndipo Mulungu wa mtendere adzakhala pamodzi ndi inu. Koma ndinakondwera mwa Ambuye kwakukulu, kuti tsopano munatsitsimukanso kulingirira mtima za kwa ine, kumenekonso munalingirirako, koma munasowa pochitapo. Si kuti ndinena monga mwa chiperewero, pakuti ndaphunzira ine, kuti zindikwanire zilizonse ndili nazo. Ndadziwa ngakhale kupeputsidwa, ndadziwanso kusefukira; konseko ndi m'zinthu zonse ndalowa mwambo wakukhuta, ndiponso wakumva njala; wakusefukira, ndiponso wakusowa. Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo. Koma munachita bwino kuti munayanjana nane m'chisautso changa. Koma mudziwanso inu nokha, inu Afilipi, kuti m'chiyambi cha Uthenga Wabwino, pamene ndinachoka kutuluka m'Masedoniya, sunayanjana nane Mpingo umodzi wonse m'makhalidwe a chopereka ndi cholandira, koma inu nokha; pakuti m'Tesalonikanso munanditumizira pa chosowa changa kamodzi kapena kawiri. Sikunena kuti nditsata choperekacho, komatu nditsata chipatso chakuchulukira ku chiwerengero chanu. Koma ndili nazo zonse, ndipo ndisefukira; ndadzazidwa, popeza ndalandira kwa Epafrodito zija zidachokera kwanu, mnunkho wa fundo labwino, nsembe yolandirika, yokondweretsa Mulungu. Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake m'ulemerero mwa Khristu Yesu. Ndipo kwa Mulungu ndi Atate wathu kukhale ulemerero kunthawi za nthawi, Amen. Lankhulani woyera mtima aliyense mwa Khristu Yesu. Abalewo akukhala ndi ine alankhula inu. Oyera mtima onse alankhula inu, koma makamaka iwo a banja la Kaisara. Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wanu. Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa chifuniro cha Mulungu, ndi Timoteo mbaleyo, kwa oyera mtima ndi abale okhulupirika mwa Khristu a m'Kolose: Chisomo kwa inu ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu. Tiyamika Mulungu Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu ndi kupempherera inu nthawi zonse, popeza tidamva za chikhulupiriro chanu cha mwa Khristu Yesu, ndi chikondi muli nacho kwa oyera mtima onse; chifukwa cha chiyembekezo chosungikira kwa inu m'Mwamba, chimene mudachimva kale m'mau a choonadi cha Uthenga Wabwino, umene udafikira kwa inu; monganso m'dziko lonse lapansi umabala zipatso, numakula, monganso mwa inu, kuyambira tsikulo mudamva nimunazindikira chisomo cha Mulungu m'choonadi; monga momwe munaphunzira kwa Epafra kapolo mnzathu wokondedwa, ndiye mtumiki wokhulupirika wa Khristu chifukwa cha ife; amenenso anatifotokozera chikondi chanu mwa Mzimu. Mwa ichi ifenso, kuyambira tsiku limene tidamva, sitileka kupembedzera ndi kupempherera inu, kuti mukadzazidwe ndi chizindikiritso cha chifuniro chake mu nzeru zonse ndi chidziwitso cha mzimu, kuti mukayenda koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m'chizindikiritso cha Mulungu; olimbikitsidwa m'chilimbiko chonse, monga mwa mphamvu ya ulemerero wake, kuchitira chipiriro chonse ndi kuleza mtima konse pamodzi ndi chimwemwe, ndi kuyamika Atate, amene anatiyeneretsa ife kulandirana nao cholowa cha oyera mtima m'kuunika; amene anatilanditsa ife kuulamuliro wa mdima, natisunthitsa kutilowetsa m'ufumu wa Mwana wa chikondi chake; amene tili nao maomboledwe mwa Iye, m'kukhululukidwa kwa zochimwa zathu; amene ali fanizo la Mulungu wosaonekayo, wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse; pakuti mwa Iye, zinalengedwa zonse za m'mwamba, ndi za padziko, zooneka ndi zosaonekazo, kapena mipando yachifumu, kapena maufumu, kapena maukulu, kapena maulamuliro; zinthu zonse zinalengedwa mwa Iye ndi kwa Iye. Ndipo Iye ali woyamba wa zonse, ndipo zonse zigwirizana pamodzi mwa Iye. Ndipo Iye ali mutu wa thupi, Mpingowo; ndiye chiyambi, wobadwa woyamba wotuluka mwa akufa; kuti akakhale Iye mwa zonse woyambayamba. Pakuti kunamkomera Atate kuti mwa Iye chidzalo chonse chikhalire, mwa Iyenso kuyanjanitsa zinthu zonse kwa Iye mwini, atachita mtendere mwa mwazi wa mtanda wake; mwa Iyetu, kapena za padziko, kapena za m'Mwamba. Ndipo inu, okhala alendo kale ndi adani m'chifuwa chanu m'ntchito zoipazo, koma tsopano anakuyanjanitsani m'thupi lake mwa imfayo, kukaimika inu oyera, ndi opanda chilema ndi osatsutsika pamaso pake; ngatitu, mukhalabe m'chikhulupiriro, ochilimika ndi okhazikika ndi osasunthika kulekana nacho chiyembekezo cha Uthenga Wabwino umene mudaumva, wolalikidwa cholengedwa chonse cha pansi pa thambo; umene ine Paulo ndakhala mtumiki wake. Tsopano ndikondwera nazo zowawazo chifukwa cha inu, ndipo ndikwaniritsa zoperewera za chisautso cha Khristu m'thupi langa chifukwa cha thupi lake, ndilo Mpingowo; amene ndinakhala mtumiki wake, monga mwa udindo wa Mulungu umene anandipatsa ine wakuchitira inu, wakukwaniritsa mau a Mulungu, ndiwo chinsinsicho chinabisika kuyambira pa nthawizo, ndi kuyambira pa mibadwoyo; koma anachionetsa tsopano kwa oyera mtima ake, kwa iwo amene Mulungu anafuna kuwazindikiritsa ichi chimene chili chuma cha ulemerero wa chinsinsi pakati pa amitundu, ndiye Khristu mwa inu, chiyembekezo cha ulemerero; amene timlalikira ife, ndi kuchenjeza munthu aliyense ndi kuphunzitsa munthu aliyense mu nzeru zonse, kuti tionetsere munthu aliyense wamphumphu mwa Khristu; kuchita ichi ndidzivutitsa ndi kuyesetsa monga mwa machitidwe ake akuchita mwa ine ndi mphamvu. Pakuti ndifuna kuti inu mudziwe nkhawa imene ndili nayo chifukwa cha inu, ndi iwowa a m'Laodikea, ndi onse amene sanaone nkhope yanga m'thupi; kuti itonthozeke mitima yao, nalumikizike pamodzi iwo m'chikondi, kufikira chuma chonse cha chidzalo cha chidziwitso, kuti akazindikire iwo chinsinsi cha Mulungu, ndiye Khristu, amene zolemera zonse za nzeru ndi chidziwitso zibisika mwa Iye. Ichi ndinena, kuti munthu asakusokeretseni inu ndi mau okopakopa. Pakuti ndingakhale ndili kwina m'thupi, komatu mumzimu ndili pamodzi ndi inu, wokondwera pakupenya makonzedwe anu, ndi chilimbiko cha chikhulupiriro chanu cha kwa Khristu. Chifukwa chake monga momwe munalandira Khristu Yesu Ambuye, muyende mwa Iye, ozika mizu ndi omangirika mwa Iye, ndi okhazikika m'chikhulupiriro, monga munaphunzitsidwa, ndi kuchulukitsa chiyamiko. Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Khristu; pakuti mwa Iye chikhalira chidzalo cha Umulungu m'thupi, ndipo muli odzazidwa mwa Iye, ndiye mutu wa ukulu wonse ndi ulamuliro; amenenso munadulidwa mwa Iye ndi mdulidwe wosachitika ndi manja, m'mavulidwe a thupi, mu mdulidwe wa Khristu; popeza munaikidwa m'manda pamodzi ndi Iye muubatizo, momwemonso munaukitsidwa pamodzi ndi Iye m'chikhulupiriro cha machitidwe a Mulungu, amene anamuukitsa Iye kwa akufa. Ndipo inu, pokhala akufa m'zolakwa ndi kusadulidwa kwa thupi lanu, anakupatsani moyo pamodzi ndi Iye, m'mene adatikhululukira ife zolakwa zonse; adatha kutifafanizira cha pa ifecho cholembedwa m'zoikikazo, chimene chinali chotsutsana nafe: ndipo anachichotsera pakatipo, ndi kuchikhomera ichi pamtanda; atavula maukulu ndi maulamuliro, anawaonetsera poyera, nawagonjetsera nako. Chifukwa chake munthu aliyense asakuweruzeni inu m'chakudya, kapena chakumwa, kapena m'kunena tsiku la chikondwerero, kapena tsiku lokhala mwezi, kapena la Sabata; ndizo mthunzi wa zilinkudzazo; koma thupi ndi la Khristu. Munthu aliyense asakunyengeni ndi kulanda mphotho yanu ndi kudzichepetsa mwini wake, ndi kugwadira kwa angelo, ndi kukhalira mu izi adaziona, wodzitukumula chabe ndi zolingalira za thupi lake, wosagwiritsa mutuwo, kuchokera kwa Iye amene thupi lonse, lothandizidwa ndi kulumikizidwa pamodzi mwa mfundo ndi mitsempha, likula ndi makulidwe a Mulungu. Ngati munafa pamodzi ndi Khristu kusiyana nazo zoyamba za dziko lapansi, mugonjeranji kuzoikikazo, monga ngati moyo wanu mukhala nao m'dziko lapansi, usaikapo dzanja, usalawa, usakhudza, (ndizo zonse zakuonongedwa pochita nazo), monga mwa malangizo ndi maphunziro a anthu? Zimene zili naotu manenedwe a nzeru m'kutumikira kwa chifuniro cha mwini wake, ndi kudzichepetsa, ndi kusalabadira thupi; koma zilibe mphamvu konse yakuletsa chikhutitso cha thupi. Chifukwa chake ngati munaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, funani zakumwamba, kumene kuli Khristu wokhala pa dzanja lamanja la Mulungu. Lingalirani zakumwamba osati za padziko ai. Pakuti munafa, ndipo moyo wanu wabisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu. Pamene Khristu adzaoneka, ndiye moyo wathu, pamenepo inunso mudzaonekera pamodzi ndi Iye m'ulemerero. Chifukwa chake fetsani ziwalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso chamanyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano; chifukwa cha izi zomwe ukudza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera; zimene munayendamo inunso kale, pamene munakhala ndi moyo wanu m'menemo. Koma tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zotuluka m'kamwa mwanu: musamanamizana wina ndi mnzake; popeza mudavula munthu wakale pamodzi ndi ntchito zake, ndipo munavala watsopano, amene alikukonzeka watsopano, kuti akhale nacho chizindikiritso, monga mwa chifaniziro cha Iye amene anamlenga iye; pamene palibe Mgriki ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, watchedwa wakunja, Mskuti, kapolo, mfulu, komatu Khristu ndiye zonse, ndi m'zonse. Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso; koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu. Ndipo mtendere wa Khristu uchite ufumu m'mitima yanu, kulingakonso munaitanidwa m'thupi limodzi; ndipo khalani akuyamika. Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalmo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu. Ndipo chilichonse mukachichita m'mau kapena muntchito, chitani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa Iye. Akazi inu, muzimvera amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye. Amuna inu, kondani akazi anu, ndipo musawawire mtima iwo. Ana inu, mverani akubala inu m'zonse, pakuti ichi Ambuye akondwera nacho. Atate inu, musaputa ana anu, kuti angataye mtima. Akapolo inu, mverani m'zonse iwo amene ali ambuye monga mwa thupi, wosati ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu ndi mtima wakulinga kumodzi, akuopa Ambuye; chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ai; podziwa kuti mudzalandira kwa Ambuye mphotho ya cholowa; mutumikira Ambuye Khristu mwaukapolo. Pakuti iye wakuchita chosalungama adzalandiranso chosalungama anachitacho; ndipo palibe tsankho. Ambuye inu, chitirani akapolo anu cholungama ndi cholingana; podziwa kuti inunso muli naye Mbuye m'Mwamba. Chitani khama m'kupemphera, nimudikire momwemo ndi chiyamiko; ndi kutipempherera ifenso pomwepo, kuti Mulungu atitsegulire ife pakhomo pa mau, kuti tilankhule chinsinsi cha Khristu; chimenenso ndikhalira m'ndende, kuti ndichionetse ichi monga ndiyenera kulankhula. Muyendere munzeru ndi iwo akunja, kuchita machawi nthawi ingatayike. Mau anu akhale m'chisomo, okoleretsa, kuti mukadziwe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani. Zonse za kwa ine adzakuzindikiritsani Tikiko, mbale wokondedwa ndi mtumiki wokhulupirika ndi kapolo mnzanga mwa Ambuye: amene ndamtuma kwa inu chifukwa cha ichi chomwe, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti atonthoze mitima yanu; pamodzi ndi Onesimo, mbale wokhulupirika ndi wokondedwa, amene ali wa kwa inu. Zonse za kuno adzakuzindikiritsani inu. Aristariko wam'ndende mnzanga akupatsani moni, ndi Marko, msuweni wa Barnabasi (amene munalandira zolamulira za kwa iye; akafika kwanu, mumlandire iye), ndi Yesu, wotchedwa Yusto, ndiwo a mdulidwe; iwo okha ndiwo antchito anzanga a mu Ufumu wa Mulungu, ndiwo akundikhalira ine chonditonthoza mtima. Akupatsani moni Epafra ndiye wa kwa inu, ndiye kapolo wa Khristu Yesu, wakulimbira chifukwa cha inu m'mapemphero ake masiku onse, kuti mukaime amphumphu ndi odzazidwa m'chifuniro chonse cha Mulungu. Pakuti ndimchitira iye umboni kuti adziwawitsa nayo ntchito chifukwa cha inu, ndi iwo a m'Laodikea, ndi iwo a m'Hierapoli. Akupatsani moni Luka sing'anga wokondedwa, ndi Dema. Akupatsani moni abalewo a m'Laodikea, ndi Nimfa, ndi Mpingowo wa m'nyumba yao. Ndipo pamene mudamwerenga kalata uyu, amwerengenso mu Mpingo wa ku Laodikea, ndi inunso muwerenge wa ku Laodikea. Ndipo nenani kwa Arkipo, Samaliratu utumiki umene udaulandira mwa Ambuye, kuti uukwanitse. Ndipereka moni ndi dzanja langa, kwa ine Paulo. Kumbukirani zomangira zanga. Chisomo chikhale nanu. Paulo, ndi Silivano, ndi Timoteo, kwa Mpingo wa Atesalonika mwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu: Chisomo kwa inu ndi mtendere. Tiyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu nonse, ndi kukumbukira inu m'mapemphero athu; ndi kukumbukira kosalekeza ntchito yanu ya chikhulupiriro, ndi chikondi chochitachita, ndi chipiriro cha chiyembekezo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu Atate wathu; podziwa, abale okondedwa ndi Mulungu, chisankhidwe chanu, kuti Uthenga Wabwino wathu sunadza kwa inu m'mau mokha, komatunso mumphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera, ndi m'kuchuluka kwakukulu; monga mudziwa tinakhala onga otani mwa inu chifukwa cha inu. Ndipo munayamba kukhala akutsanza athu, ndi a Ambuye, m'mene mudalandira mauwo m'chisautso chambiri, ndi chimwemwe cha Mzimu Woyera; kotero kuti munayamba kukhala inu chitsanzo kwa onse akukhulupirira m'Masedoniya ndi m'Akaya. Pakuti kutuluka kwa inu kudamveka mau a Ambuye, osati m'Masedoniya ndi Akaya mokha, komatu m'malo monse chikhulupiriro chanu cha kwa Mulungu chidatuluka; kotero kuti sikufunika kwa ife kulankhula kanthu. Pakuti iwo okha alalikira za ife, malowedwe athu a kwa inu anali otani; ndi kuti munatembenukira kwa Mulungu posiyana nao mafano, kutumikira Mulungu weniweni wamoyo, ndi kulindirira Mwana wake achokere Kumwamba, amene anamuukitsa kwa akufa, Yesu, wotipulumutsa ife kumkwiyo ulinkudza. Pakuti, abale, mudziwa nokha malowedwe athu a kwa inu, kuti sanakhala opanda pake; koma tingakhale tidamva zowawa kale, ndipo anatichitira chipongwe, monga mudziwa, ku Filipi, tinalimbika pakamwa mwa Mulungu wathu kulankhula ndi inu Uthenga Wabwino wa Mulungu m'kutsutsana kwambiri. Pakuti kudandaulira kwathu sikuchokera kukusochera, kapena kuchidetso, kapena m'chinyengo; komatu monga Mulungu anativomereza kutiikiza Uthenga Wabwino, kotero tilankhula; osati monga okondweretsa anthu, koma Mulungu; amene ayesa mitima yathu. Pakuti sitinayenda nao mau osyasyalika nthawi iliyonse monga mudziwa, kapena kupsinjika msiriro, mboni ndi Mulungu; kapena sitinakhala ofuna ulemerero wa kwa anthu, kapena kwa inu, kapena kwa ena, tingakhale tinali nayo mphamvu yakukulemetsani monga atumwi a Khristu. Komatu tinakhala ofatsa pakati pa inu, monga m'mene mlezi afukata ana ake a iye yekha; kotero ife poliralira inu, tinavomera mokondwera kupereka kwa inu si Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso moyo wathu, popeza mudakhala okondedwa kwa ife. Pakuti mukumbukira, abale, chigwiritso chathu ndi chivuto chathu; pochita usiku ndi usana, kuti tingalemetse wina wa inu, tinalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu. Inu ndinu mboni, Mulungunso, kuti tinakhala oyera mtima ndi olungama ndi osalakwa kwa inu akukhulupirira; monga mudziwa kuti tinachitira yense wa inu pa yekha, monga atate achitira ana ake a iye yekha, ndi kukudandaulirani, ndi kukusangalatsani ndi kuchita umboni, kuti muyende koyenera Mulungu, amene akuitanani inu mulowe ufumu wake wa Iye yekha, ndi ulemerero. Ndipo mwa ichinso ife tiyamika Mulungu kosalekeza, kuti, pakulandira mau a Uthenga wa Mulungu, simunawalandira monga mau a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mau a Mulungu, amenenso achita mwa inu okhulupirira. Pakuti inu, abale, munayamba kukhala akutsanza a Mipingo ya Mulungu yokhala m'Yudeya mwa Khristu Yesu; popeza zomwezi mudazimva kowawa ndinunso pamanja pa a mtundu wanu wa inu nokha, monganso iwowa pa manja a Ayuda; amene adaphanso Ambuye Yesu, ndi aneneri, natilondalonda ife, ndipo sakondweretsa Mulungu, natsutsana nao anthu onse; natiletsa ife kuti tisalankhule ndi akunja kuti apulumutsidwe; kudzaza machimo ao nthawi zonse; koma mkwiyo wafika pa iwo kufikira chimaliziro. Koma ife, abale, angakhale adatichotsa kusiyana nanu kanthawi, osapenyana maso, koma kusiyana mtima ai, tinayesetsa koposa kuona nkhope yanu ndi chilakolako chachikulu; chifukwa tinafuna kudza kwa inu, inedi Paulo ndatero kamodzi kapena kawiri; koma Satana anatiletsa. Pakuti chiyembekezo chathu, kapena chimwemwe, kapena korona wakudzitamandira naye nchiyani? Si ndinu nanga, pamaso pa Ambuye wathu Yesu m'kufika kwake? Pakuti inu ndinu ulemerero wathu ndi chimwemwe chathu. Chifukwa chake, posakhoza kulekereranso, tidavomereza mtima atisiye tokha ku Atene; ndipo tinatuma Timoteo, mbale wathuyo ndi mtumiki wa Mulungu m'Uthenga Wabwino wa Khristu, kuti akhazikitse inu, ndi kutonthoza inu za chikhulupiriro chanu; kuti asasunthike wina ndi zisautso izi, pakuti mudziwa nokha kuti adatiika ife tichite izi. Pakutinso, pamene tinali ndi inu tinakuuziranitu kuti tidzamva zisautso; monga kudachitika, monganso mudziwa. Mwa ichi inenso, posalekereranso, ndinatuma kukazindikira chikhulupiriro chanu, kuti kapena woyesa akadakuyesani, ndipo chivuto chathu chikadakhala chopanda pake. Koma tsopano pofika Timoteo kwathu kuchokera kwa inu, ndi kutifotokozera mbiri yokoma ya chikhulupiriro ndi chikondano chanu, ndi kuti mutikumbukira bwino masiku onse, pokhumba kutiona ife, monganso ife kukuonani inu; chifukwa cha ichi tasangalala pa inu, abale, m'kupsinjika kwathu konse ndi chisautso chathu chonse, mwa chikhulupiriro chanu; pakuti tsopano tili ndi moyo, ngati inu muchilimika mwa Ambuye. Pakuti tikhoza kubwezera kwa Mulungu chiyamiko chanji chifukwa cha inu, pa chimwemwe chonse tikondwera nacho mwa inu pamaso pa Mulungu wathu; ndi kuchulukitsa mapemphero athu usiku ndi usana kuti tikaone nkhope yanu, ndi kukwaniritsa zoperewera pa chikhulupiriro chanu? Koma Mulungu Atate wathu mwini yekha, ndi Ambuye wathu Yesu atitsogolere m'njira yakufika kwa inu; koma Ambuye akukulitseni inu, nakuchulukitseni m'chikondano wina kwa mnzake ndi kwa anthu onse, monganso ife titero kwa inu; kuti akakhazikitse mitima yanu yopanda chifukwa m'chiyero pamaso pa Mulungu Atate wathu, pakufika Ambuye wathu Yesu pamodzi ndi oyera mtima ake onse. Chotsalira tsono, abale, tikupemphani ndi kukudandaulirani mwa Ambuye Yesu, kuti, monga munalandira kwa ife mayendedwe okoma, muyenera kuyendanso ndi kukondweretsa Mulungu, monganso mumayenda, chulukani koposa momwemo. Pakuti mudziwa malangizo amene tinakupatsani mwa Ambuye Yesu. Pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu, chiyeretso chanu, kuti mudzipatule kudama; yense wa inu adziwe kukhala nacho chotengera chake m'chiyeretso ndi ulemu, kosati m'chiliro cha chilakolako chonyansa, monganso amitundu osadziwa Mulungu; asapitirireko munthu, nanyenge mbale wake m'menemo, chifukwa Ambuye ndiye wobwezera wa izi zonse, monganso tinakuuziranitu, ndipo tinachitapo umboni. Pakuti Mulungu sanaitana ife titsate chidetso, koma chiyeretso. Chifukwa chake iye wotaya ichi, sataya munthu, komatu Mulungu, wakupatsa Mzimu wake Woyera kwa inu. Koma kunena za chikondano cha pa abale sikufunika kuti akulembereni; pakuti wakukuphunzitsani ndi Mulungu, kuti mukondane wina ndi mnzake; pakutinso munawachitira ichi abale onse a m'Masedoniya lonse. Koma tikudandaulirani, abale, muchulukireko koposa, ndi kuti muyesetse kukhala chete ndi kuchita za inu eni ndi kugwira ntchito ndi manja anu, monga tinakuuzani; kuti mukayende oona mtima pa iwo a kunja, ndi kukhala osasowa kanthu. Koma sitifuna, abale, kuti mukhale osadziwa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo. Pakuti ngati tikhulupirira kuti Yesu adamwalira, nauka, koteronso Mulungu adzatenga pamodzi ndi Iye iwo akugona mwa Yesu. Pakuti ichi tinena kwa inu m'mau a Ambuye, kuti ife okhala ndi moyo, otsalira kufikira kufikanso kwa Ambuye, sitidzatsogolera ogonawo. Pakuti Ambuye adzatsika Kumwamba mwini yekha ndi mfuu, ndi mau a mngelo wamkulu, ndi lipenga la Mulungu; ndipo akufa mwa Khristu adzayamba kuuka; pamenepo ife okhala ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa nao pamodzi m'mitambo, kukakomana ndi Ambuye mumlengalenga, ndipo potero tidzakhala ndi Ambuye nthawi zonse. Chomwecho, tonthozanani ndi mau awa. Koma za nthawizo ndi nyengozo, abale, sikufunika kuti tidzakulemberani. Pakuti inu nokha mudziwa bwino kuti tsiku la Ambuye lidzadza monga mbala usiku. Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo chionongeko chobukapo chidzawagwera, monga zowawa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse. Koma inu, abale, simuli mumdima, kuti tsikulo likakugwereni monga mbala; pakuti inu nonse muli ana a kuunika, ndi ana a usana; sitili a usiku, kapena a mdima; chifukwa chake tsono tisagone monga otsalawo, komatu tidikire, ndipo tisaledzere. Pakuti iwo akugona agona usiku; ndi iwo akuledzera aledzera usiku. Koma ife popeza tili a usana tisaledzere, titavala chapachifuwa cha chikhulupiriro ndi chikondi; ndi chisoti chili chiyembekezo cha chipulumutso. Pakuti Mulungu sanatiika ife tilawe mkwiyo, komatu kuti tilandire chipulumutso mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anafa m'malo mwathu, kuti, tingakhale tidikira, tingakhale tigona, tikakhale ndi moyo pamodzi ndi Iye. Mwa ichi chenjezanani, ndipo mangiriranani wina ndi mnzake, monganso mumachita. Koma, abale, tikupemphani, dziwani iwo akugwiritsa ntchito mwa inu, nakhala akulu anu mwa Ambuye, nakuyambirirani inu; ndipo muwachitire ulemu woposatu mwa chikondi, chifukwa cha ntchito yao. Khalani mumtendere mwa inu nokha. Koma tidandaulira inu abale, yambirirani amphwayi, limbikitsani amantha mtima? Chirikizani ofooka, mukhale oleza mtima pa onse. Penyani kuti wina asabwezere choipa womchitira choipa; komatu nthawi zonse mutsatire chokoma, kwa anzanu, ndi kwa onse. Kondwerani nthawi zonse; Pempherani kosaleka; M'zonse yamikani; pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu cha kwa inu, mwa Khristu Yesu. Musazime Mzimuyo; Musanyoze manenero; Yesani zonse; sungani chokomacho, Mupewe maonekedwe onse a choipa. Ndipo Mulungu wa mtendere yekha ayeretse inu konsekonse; ndipo mzimu wanu ndi moyo wanu ndi thupi lanu zisungidwe zamphumphu, zopanda chilema pa kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu. Wakuitana inu ali wokhulupirika, amenenso adzachichita. Abale, tipempherereni ife. Perekani moni kwa abale onse ndi chipsompsono chopatulika. Ndikulumbirirani pa Ambuye kuti kalatayu awerengedwe kwa abale onse. Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale nanu. Paulo, ndi Silivano, ndi Timoteo, kwa Mpingo wa Atesalonika mwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu: Chisomo kwa inu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu. Tiziyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale, monga kuyenera; pakuti chikhulupiriro chanu chikula chikulire, ndipo chichulukira chikondano cha inu nonse, yense pa mnzake; kotero kuti ife tokha tidzitamandira za inu m'Mipingo ya Mulungu, chifukwa cha chipiriro chanu, ndi chikhulupiriro chanu, m'mazunzo anu onse ndi zisautsozo muzimva; ndicho chitsimikizo cha chiweruziro cholungama cha Mulungu; kuti mukawerengedwe oyenera ufumu wa Mulungu, umenenso mumvera zowawa; popeza nkolungama kwa Mulungu kubwezera chisautso kwa iwo akuchitira inu chisautso, ndi kwa inu akumva chisautso mpumulo pamodzi ndi ife, pa vumbulutso la Ambuye Yesu wochokera Kumwamba pamodzi ndi angelo a mphamvu yake, m'lawi lamoto, ndi kubwezera chilango kwa iwo osamdziwa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu; amene adzamva chilango, ndicho chionongeko chosatha chowasiyanitsa kunkhope ya Ambuye, ndi kuulemerero wa mphamvu yake, pamene adzadza kudzalemekezedwa mwa oyera mtima ake, ndi kukhala wodabwizitsa mwa onse akukhulupirira (popeza munakhulupirira umboni wathu wa kwa inu) m'tsiku lija. Kukatero tikupemphereraninso nthawi zonse, kuti Mulungu wathu akakuyeseni inu oyenera kuitanidwa kwanu, nakakwaniritse chomkomera chonse, ndi ntchito ya chikhulupiriro mumphamvu; kuti dzina la Ambuye wathu Yesu lilemekezedwe mwa inu, ndi inu mwa Iye, monga mwa chisomo cha Mulungu wathu ndi Ambuye Yesu Khristu. Ndipo tikupemphani, abale, chifukwa cha kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi kusonkhana pamodzi kwathu kwa Iye; kuti musamagwedezeka mtima msanga ndi kutaya maganizo anu, kapena kuopsedwa, mwa mzimu kapena mwa mau; kapena mwa kalata, monga wolembedwa ndi ife, monga ngati tsiku la Ambuye lafika; munthu asakunyengeni konseko; kuti silifika, koma chiyambe chifike chipatukocho, navumbulutsike munthu wosaweruzika, mwana wa chionongeko, amene atsutsana nazo, nadzikuza pa zonse zotchedwa Mulungu, kapena zopembedzeka; kotero kuti iye wakhala pansi ku Kachisi wa Mulungu, nadzionetsera yekha kuti ali Mulungu. Simukumbukira kodi, kuti pokhala nanu, ndisanachoke ine, ndinakuuzani izi? Ndipo tsopano chomletsa muchidziwa, kuti akavumbulitsidwe iye m'nyengo yake ya iye yekha. Pakuti chinsinsi cha kusaweruzika chayambadi kuchita; chokhachi pali womletsa tsopano, kufikira akamchotsa pakati. Ndipo pamenepo adzavumbulutsidwa wosaweruzikayo, amene Ambuye Yesu adzamthera ndi mzimu wa pakamwa pake, nadzamuononga ndi maonekedwe a kudza kwake; ndiye amene kudza kwake kuli monga mwa machitidwe a Satana, mu mphamvu yonse, ndi zizindikiro ndi zozizwa zonama; ndi m'chinyengo chonse cha chosalungama kwa iwo akuonongeka, popeza chikondi cha choonadi sanachilandira, kuti akapulumutsidwe iwo. Ndipo chifukwa chake Mulungu atumiza kwa iwo machitidwe a kusocheretsa, kuti akhulupirire bodza; kuti aweruzidwe onse amene sanakhulupirira choonadi, komatu anakondwera ndi chosalungama. Koma tiyenera ife tiziyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale okondedwa ndi Ambuye, kuti Mulungu anakusankhani inu kuyambira pachiyambi, mulandire chipulumutso mwa chiyeretso cha Mzimu ndi chikhulupiriro cha choonadi; kumene anaitanako inu mwa Uthenga Wabwino wathu, kuti mulandire ulemerero wa Ambuye wathu Yesu Khristu. Chifukwa chake tsono, abale, chilimikani, gwiritsani miyambo imene tinakuphunzitsani, kapena mwa mau, kapena mwa kalata wathu. Ndipo Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi Mulungu Atate wathu amene anatikonda natipatsa chisangalatso chosatha ndi chiyembekezo chokoma mwa chisomo, asangalatse mitima yanu, nakhazikitse inu mu ntchito yonse ndi mau onse abwino. Chotsalira, abale, mutipempherere, kuti mau a Ambuye athamange, nalemekezedwe, monganso kwanu; ndi kuti tilanditsidwe m'manja a anthu osayenera ndi oipa; pakuti si onse ali nacho chikhulupiriro. Koma Ambuye ali wokhulupirika amene adzakukhazikitsani inu, nadzakudikirirani kuletsa woipayo; koma tikhulupirira mwa Ambuye za inu, kuti mumachita, ndiponso mudzachita zimene tikulamulirani. Ndipo Ambuye atsogolere bwino mitima yanu ilowe m'chikondi cha mulungu ndi m'chipiriro cha Khristu. Ndipo tikulamulirani, abale, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti mubwevuke kwa mbale yense wakuyenda dwakedwake, wosatsata mwambo umene anaulandira kwa ife. Pakuti mudziwa nokha m'mene muyenera kutitsanza ifemo; pakuti sitinakhala dwakedwake mwa inu; kapena sitinadya mkate chabe pa dzanja la munthu aliyense, komatu m'chivuto ndi chipsinjo, tinagwira ntchito usiku ndi usana, kuti tingalemetse wina wa inu; si chifukwa tilibe ulamuliro, komatu kuti tidzipereke tokha tikhale kwa inu chitsanzo chanu, kuti mukatitsanze ife. Pakutinso pamene tinali nanu tidakulamulirani ichi, Ngati munthu safuna kugwira ntchito, asadyenso. Pakuti tikumva za ena mwa inu kuti ayenda dwakedwake, osagwira ntchito konse, koma ali ochita mwina ndi mwina. Koma oterewa tiwalamulira ndi kuwadandaulira mwa Ambuye Yesu Khristu, kuti agwire ntchito pokhala chete, nadye chakudya cha iwo okha. Koma inu, abale, musaleme pakuchita zabwino. Koma ngati wina samvera mau athu m'kalata uyu, yang'anirani ameneyo, kuti musayanjane naye, kuti achite manyazi. Koma musamuyese mdani, koma mumuyambirire ngati mbale. Ndipo Ambuye wa mtendere yekha atipatse ife mtendere nthawi zonse, monsemo. Ambuye akhale ndi inu nonse. Ndipereka moni ndi dzanja langa Paulo; ndicho chizindikiro m'kalata aliyense; ndiko kulemba kwanga. Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse. Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu monga mwa chilamuliro cha Mulungu Mpulumutsi wathu, ndi cha Khristu Yesu, chiyembekezo chathu: kwa Timoteo mwana wanga weniweni m'chikhulupiriro: Chisomo, chifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi kwa Khristu Yesu Ambuye wathu. Monga ndinakudandaulira iwe utsalire m'Efeso, popita ine ku Masedoniya, nditeronso, kuti ukalamulire ena ajawa asaphunzitse kanthu kena, kapena asasamale nkhani zachabe, ndi mawerengedwe osalekeza a mafuko a makolo, ndiwo akuutsa mafunso, osati za udindo wa Mulungu umene uli m'chikhulupiriro; koma chitsirizo cha chilamuliro ndicho chikondi chochokera mu mtima woyera ndi m'chikumbu mtima chokoma ndi chikhulupiriro chosanyenga; zimenezo, ena pozilambalala anapatukira kutsata mau opanda pake; pofuna kukhala aphunzitsi a malamulo ngakhale sadziwitsa zimene azinena, kapena azilimbikirazi. Koma mudziwa kuti lamulo ndi labwino, ngati munthu achita nalo monga mwa lamulo, podziwa ichi, kuti lamulo siliikika kwa munthu wolungama, koma kwa osaweruzika ndi osamvera lamulo, osapembedza, ndi ochimwa, osalemekeza ndi amnyozo, akupha atate ndi akupha amai, akupha anzao, achigololo, akuchita zoipa ndi amuna, akuba anthu, amabodza, olumbira zonama, ndipo ngati kuli kena kakutsutsana nacho chiphunzitso cholamitsa; monga mwa Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Mulungu wolemekezeka, umene anandisungitsa ine. Ndimyamika Iye wondipatsa ine mphamvu, ndiye Khristu Yesu, Ambuye wathu, kuti anandiyesa wokhulupirika, nandiika kuutumiki, ndingakhale kale ndinali wamwano, ndi wolondalonda, ndi wachipongwe; komatu anandichitira chifundo, popeza ndinazichita wosazindikira, wosakhulupirira; koma chisomo cha Ambuye wathu chidachulukatu pamodzi ndi chikhulupiriro ndi chikondi chili mwa Khristu Yesu. Mauwa ali okhulupirika ndi oyenera konse kuti awalandire, kuti Khristu Yesu anadza kudziko lapansi kupulumutsa ochimwa; wa iwowa ine ndine woposa; komatu mwa ichi anandichitira chifundo, kuti mwa ine, woyamba, Yesu Khristu akaonetsere kuleza mtima kwake konse kukhale chitsanzo cha kwa iwo adzakhulupirira pa Iye m'tsogolo kufikira moyo wosatha. Ndipo kwa Mfumu yosatha, yosavunda, yosaoneka, Mulungu wa yekha, ukhale ulemu ndi ulemerero, kufikira nthawi za nthawi. Amen. Lamulo ili ndipereka kwa iwe, mwana wanga Timoteo, kuti, monga mwa zonenera zidakutsogolera iwe kale, ulimbane nayo nkhondo yabwino; ndi kukhala nacho chikhulupiriro ndi chikumbu mtima chokoma, chimene ena adachikankha, chikhulupiriro chao chidatayika; a iwo ali Himeneo ndi Aleksandro, amene ndawapereka kwa Satana, kuti aphunzire kusalankhula zamwano. Ndidandaulira tsono, poyambayamba, kuti achitike mapembedzo, mapemphero, mapembedzero, mayamiko, chifukwa cha anthu onse; chifukwa cha mafumu ndi onse akuchita ulamuliro; kuti m'moyo mwathu tikakhale odika mtima ndi achete m'kulemekeza Mulungu, ndi m'kulemekezeka monse. Pakuti ichi nchokoma ndi cholandirika pamaso pa Mulungu Mpulumutsi wathu; amene afuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi. Pakuti pali Mulungu mmodzi, ndi Mtetezi mmodzi pakati pa Mulungu ndi anthu, ndiye munthu, Khristu Yesu, amene anadzipereka yekha chiombolo m'malo mwa onse; umboni m'nyengo zake; umene anandiika ine mlaliki wake ndi mtumwi (ndinena zoona, wosanama ine), mphunzitsi wa amitundu m'chikhulupiriro ndi choonadi. Chifukwa chake ndifuna kuti amunawo apemphere pamalo ponse, ndi kukweza manja oyera, opanda mkwiyo ndi makani. Momwemonso, akazi adziveke okha ndi chovala choyenera, ndi manyazi, ndi chidziletso; osati ndi tsitsi lake loluka, ndi golide kapena ngale, kapena malaya a mtengo wake wapatali; komatu (umo mokomera akazi akuvomereza kulemekeza Mulungu), mwa ntchito zabwino. Mkazi aphunzire akhale wachete m'kumvera konse. Koma sindilola ine kuti mkazi aphunzitse, kapena kulamulira mwamuna; komatu akhale chete. Pakuti Adamu anayamba kulengedwa, pamenepo Heva; ndipo Adamu sananyengedwa, koma mkaziyo ponyengedwa analowa m'kulakwa; koma adzapulumutsidwa mwa kubala mwana, ngati akhala m'chikhulupiriro ndi chikondi ndi chiyeretso pamodzi ndi chidziletso. Mauwa ali okhulupirika, ngati munthu akhumba udindo wa woyang'anira, aifuna ntchito yabwino. Ndipo kuyenera woyang'anira akhale wopanda chilema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wodzisunga, wodziletsa, wolongosoka, wokonda kuchereza alendo, wokhoza kuphunzitsa; wosati woledzera, kapena womenyana ndeu; komatu wofatsa, wopanda ndeu, wosakhumba chuma; woweruza bwino nyumba yake ya iye yekha, wakukhala nao ana ake omvera iye ndi kulemekezeka konse. Koma ngati munthu sadziwa kuweruza nyumba ya iye yekha, adzasunga bwanji Mpingo wa Mulungu? Asakhale wophunza, kuti podzitukumula ungamgwere mlandu wa mdierekezi. Kuyeneranso kuti iwo akunja adzakhoza kumchitira umboni wabwino; kuti ungamgwere mtonzo, ndi msampha wa mdierekezi. Momwemonso atumiki akhale olemekezeka, osanena pawiri, osamwetsa vinyo, osati a chisiriro chonyansa; okhala nacho chinsinsi cha chikhulupiriro m'chikumbu mtima choona. Koma iwonso ayamba ayesedwe; pamenepo atumikire, akakhala opanda chifukwa. Momwemonso akazi akhale olemekezeka, osadierekeza, odzisunga, okhulupirika m'zonse. Atumiki akhale mwamuna wa mkazi mmodzi, akuweruza bwino ana ao, ndi iwo a m'nyumba yao ya iwo okha. Pakuti iwo akutumikira bwino adzitengera okha mbiri yabwino, ndi kulimbika kwakukulu m'chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu. Izi ndikulembera ndi kuyembekeza kudza kwa iwe posachedwa, koma ngati ndichedwa, kuti udziwe kuyenedwa kwake pokhala m'nyumba ya Mulungu, ndiye Mpingo wa Mulungu wamoyo, mzati ndi mchirikizo wa choonadi. Ndipo povomerezeka, chinsinsi cha kuchitira Mulungu ulemu nchachikulu: Iye amene anaonekera m'thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m'dziko lapansi, wolandiridwa m'ulemerero. Koma Mzimu anena monenetsa, kuti m'masiku otsiriza ena adzataya chikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosocheretsa ndi maphunziro a ziwanda, m'maonekedwe onyenga a iwo onena mabodza, olochedwa m'chikumbu mtima mwao monga ndi chitsulo chamoto; a kuletsa ukwati, osiyitsa zakudya zakuti, zimene Mulungu anazilenga kuti achikhulupiriro ndi ozindikira choonadi azilandire ndi chiyamiko. Pakuti cholengedwa chonse cha Mulungu nchabwino, ndipo palibe kanthu kayenera kutayika, ngati kalandiridwa ndi chiyamiko; pakuti kayeretsedwa ndi Mau a Mulungu ndi kupemphera. Ngati ukumbutsa abale zinthu izi, udzakhala mtumiki wabwino wa Khristu Yesu, woleredwa m'mauwo a chikhulupiriro, ndi malangizo abwino amene udawatsata; koma nkhani zachabe ndi za akazi okalamba ukane. Ndipo udzizoloweretse kuchita chipembedzo; pakuti chizolowezi cha thupi chipindula pang'ono, koma chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la kumoyo uno, ndi la moyo ulinkudza. Okhulupirika mauwa ndi oyenera kulandiridwa konse. Pakuti kukalingako tigwiritsa ntchito ndi kuyesetsa, chifukwa chiyembekezo chathu tili nacho pa Mulungu wamoyo, amene ali Mpulumutsi wa anthu onse, makamaka wa okhulupirira. Lamulira izi, nuziphunzitse. Munthu asapeputse ubwana wako; komatu khala chitsanzo kwa iwo okhulupirira, m'mau, m'mayendedwe, m'chikondi, m'chikhulupiriro, m'kuyera mtima. Kufikira ndidza ine, usamalire kuwerenga, kuchenjeza, kulangiza. Usanyalapse mphatsoyo ili mwa iwe, yopatsidwa kwa iwe mwa chinenero, pamodzi ndi kuika kwa manja a akulu. Izi uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti kukula mtima kwako kuonekere kwa onse. Udzipenyerere wekha, ndi chiphunzitsocho. Uzikhala mu izi; pakuti pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe. Mkulu usamdzudzule, komatu umdandaulire ngati atate; anyamata ngati abale; akazi akulu ngati amai; akazi aang'ono ngati alongo, m'kuyera mtima konse. Chitira ulemu amasiye amene ali amasiye ndithu. Koma ngati wamasiye wina ali nao ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m'banja lao, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu. Koma iye amene ali wamasiye ndithu, nasiyidwa yekha, ayembekezera Mulungu, nakhalabe m'mapembedzo ndi mapemphero usiku ndi usana. Koma iye wakutsata zomkondweretsa, adafa pokhala ali ndi moyo. Ndipo izi ulamulire, kuti akhale opanda chilema. Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupirira. Asawerengedwe wamasiye ngati sanafikire zaka makumi asanu ndi limodzi, atakhala mkazi wa mwamuna mmodzi, wa mbiri ya ntchito zabwino; ngati walera ana, ngati wachereza alendo, ngati adasambitsa mapazi a oyera mtima, ngati wathandiza osautsidwa, ngati anatsatadi ntchito zonse zabwino. Koma amasiye ang'ono uwakane; pakuti pamene ayamba kumchitira Khristu chipongwe afuna kukwatiwa; pokhala nacho chitsutso, popeza adataya chikhulupiriro chao choyamba. Ndipo aphunziraponso kuchita ulesi, aderuderu; koma osati ulesi wokha, komatunso alankhula zopanda pake, nachita mwina ndi mwina, olankhula zosayenera. Chifukwa chake nditi akwatiwe amasiye ang'ono, nabale ana, naweruzire nyumba, osapatsa chifukwa kwa mdaniyo chakulalatira; pakuti adayamba ena kupatuka ndi kutsata Satana. Ngati mkazi wina wokhulupirira ali nao amasiye, iye awathandize, ndipo Mpingowo usalemedwe; kuti uthandize iwo amene ali amasiye ndithu. Akulu akuweruza bwino ayesedwe oyenera ulemu wowirikiza, makamaka iwo akuchititsa m'mau ndi m'chiphunzitso. Pakuti malembo ati, Usapunamiza ng'ombe yopuntha tirigu. Ndipo Wogwira ntchito ayenera kulipira kwake. Pa mkulu usalandire chomnenera, koma pakhale mboni ziwiri kapena zitatu. Iwo akuchimwa uwadzudzule pamaso pa onse, kuti otsalawo achite mantha. Ndikuchitira umboni pamaso pa Mulungu, ndi Khristu Yesu, ndi angelo osankhika, kuti usunge izi kopanda kusankhiratu, wosachita kanthu monga mwa tsankho. Usafulumira kuika manja pa munthu aliyense, kapena usayanjana nazo zoipa za eni; udzisunge wekha woyera mtima. Usakhalenso wakumwa madzi okha, komatu uchite naye vinyo pang'ono, chifukwa cha mimba yako ndi zofooka zako zobwera kawirikawiri. Zochimwa za anthu ena zili zooneka kale, zitsogola kunka kumlandu; koma enanso ziwatsata. Momwemonso pali ntchito zokoma zinaonekera kale; ndipo zina zosati zotere sizikhoza kubisika. Onse amene ali akapolo a m'goli, ayesere ambuye a iwo okha oyenera ulemu wonse, kuti dzina la Mulungu ndi chiphunzitso zisachitidwe mwano. Ndipo iwo akukhala nao ambuye okhulupirira, asawapeputse popeza ali abale; koma makamaka awatumikire popeza ali okhulupirira ndi okondedwa, oyanjana nao pa chokomacho. Izi uphunzitse, nuchenjeze. Ngati munthu aphunzitsa zina, wosavomerezana nao mau a moyowo a Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi chiphunzitsocho chili monga mwa chipembedzo: iyeyo watukumuka, wosadziwa kanthu, koma ayalukira pa mafunso ndi makani a mau, kumene zichokerako njiru, ndeu, zamwano, mayerekezo oipa; makani opanda pake a anthu oipsika nzeru ndi ochotseka choonadi, akuyesa kuti chipembedzo chipindulitsa. Koma chipembedzo pamodzi ndi kudekha chipindulitsa kwakukulu; pakuti sitinatenga kanthu polowa m'dziko lapansi, ndiponso sitikhoza kupita nako kanthu pochoka pano; koma pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimene zitikwanire. Koma iwo akufuna kukhala achuma amagwa m'chiyesero ndi m'msampha, ndi m'zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m'chionongeko ndi chitayiko. Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama; chimene ena pochikhumba, anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zowawa zambiri. Koma iwe, munthu wa Mulungu iwe, thawa izi; nutsate chilungamo, chipembedzo, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, chifatso. Limba nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro, gwira moyo wosatha, umene adakuitanira, ndipo wavomereza chivomerezo chabwino pamaso pa mboni zambiri. Ndikulamulira pamaso pa Mulungu, wozipatsa zinthu zonse moyo, ndi Khristu Yesu, amene anachitira umboni chivomerezo chabwino kwa Pontio Pilato; kuti usunge lamulolo, lopanda banga, lopanda chilema, kufikira maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Khristu; limene adzalionetsa m'nyengo za Iye yekha, amene ali Mwini Mphamvu wodala ndi wayekha, ndiye Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye; amene Iye yekha ali nao moyo wosatha, wakukhala m'kuunika kosakhozeka kufikako; amene munthu sanamuona, kapena sakhoza kumuona; kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu yosatha. Amen. Lamulira iwo achuma m'nthawi yino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziwika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo; kuti achite zabwino, nachuluke ndi ntchito zabwino, nakondwere kugawira ena, nayanjane; nadzikundikire okha maziko okoma ku nyengo ikudzayi, kuti akagwire moyo weniweniwo. Timoteo iwe, dikira chokusungitsa, ndi kulewa zokamba zopanda pake ndi zotsutsana za ichi chitchedwa chizindikiritso konama; chimene ena pochivomereza adalakwa ndi kutaya chikhulupiriro. Chisomo chikhale nanu. Paulo mtumwi wa Khristu Yesu mwa chifuniro cha Mulungu, monga mwa lonjezano la moyo wa m'Khristu Yesu, kwa Timoteo, mwana wanga wokondedwa: Chisomo, chifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Ambuye wathu. Ndiyamika Mulungu, amene ndimtumikira kuyambira makolo anga ndi chikumbu mtima choyera, kuti ndikumbukira iwe kosalekeza m'mapemphero anga, pokhumba usiku ndi usana kukuona iwe, ndi kukumbukira misozi yako, kuti ndidzazidwe nacho chimwemwe; pokumbukira chikhulupiriro chosanyenga chili mwa iwe, chimene chinayamba kukhala mwa mbuye wako Loisi, ndi mwa mai wako Yunisi, ndipo, ndakopeka mtima, mwa iwenso. Chifukwa chake ndikukumbutsa iwe ukoleze mphatso ya Mulungu, ili mwa iwe mwa kuika kwa manja anga. Pakuti Mulungu sanatipatsa mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso. Potero usachite manyazi pa umboni wa Ambuye wathu, kapena pa ine wandende wake; komatu umve masautso ndi Uthenga Wabwino, monga mwa mphamvu ya Mulungu; amene anatipulumutsa ife, natiitana ife ndi maitanidwe oyera, si monga mwa ntchito zathu, komatu monga mwa chitsimikizo mtima cha Iye yekha, ndi chisomo, chopatsika kwa ife mwa Khristu Yesu nthawi zisanayambe, koma chaonetsedwa tsopano m'maonekedwe a Mpulumutsi wathu Khristu Yesu, amenedi anatha imfa, naonetsera poyera moyo ndi chosavunda mwa Uthenga Wabwino, umene ndaikikapo mlaliki, ndi mtumwi ndi mphunzitsi wake. Chifukwa cha ichicho ndinamva zowawa izi; komatu sindichita manyazi; pakuti ndimdziwa Iye amene ndamkhulupirira, ndipo ndikopeka mtima kuti ali wa mphamvu ya kudikira chosungitsa changacho kufikira tsiku lijalo. Gwira chitsanzo cha mau a moyo, amene udawamva kwa ine, mwa chikhulupiriro ndi chikondi chili mwa Khristu Yesu. Chosungitsa chokomacho udikire mwa Mzimu Woyera amene akhalitsa mwa ife. Ichi uchidziwa, kuti onse a m'Asiya adabwerera kusiyana nane; a iwo ali Figelo ndi Heremogene. Ambuye achitire banja la Onesifore chifundo; pakuti anatsitsimutsa ine kawirikawiri, ndipo sanachita manyazi ndi unyolo wanga; komatu pokhala m'Roma iye anandifunafuna ine ndi khama, nandipeza. (Ambuye ampatse iye apeze chifundo ndi Ambuye tsiku lijalo); ndi muja ananditumikira m'zinthu zambiri m'Efeso, uzindikira iwe bwino. Ndipo iwe, mwana wanga, limbika m'chisomo cha m'Khristu Yesu. Ndipo zimene wazimva kwa ine mwa mboni zambiri, zomwezi uikize kwa anthu okhulupirika, amene adzadziwa kuphunzitsa enanso. Umve zowawa pamodzi nane monga msilikali wabwino wa Khristu Yesu. Msilikali sakodwa nazo ntchito wamba, kuti akakondweretse iye amene adamlemba usilikali. Koma ngatinso wina ayesana nao m'makani amasewero, samveka korona ngati sanayesana monga adapangana. Wam'munda wogwiritsitsa ntchitoyo ayenera akhale woyamba kulandira zipatsozo. Lingirira chimene ndinena; pakuti Ambuye adzakupatsa chidziwitso m'zonse. Kumbukira Yesu Khristu, wouka kwa akufa, wochokera m'mbeu ya Davide, monga mwa Uthenga Wabwino wanga; m'menemo ndimva zowawa kufikira zomangira, monga wochita zoipa; koma mau a Mulungu samangika. Mwa ichi ndipirira zonse, chifukwa cha osankhika, kuti iwonso akapeze chipulumutsocho cha mwa Khristu Yesu, pamodzi ndi ulemerero wosatha. Okhulupirika mauwa: Pakuti ngati tidamwalira ndi Iye, tidzakhalanso moyo ndi Iye: ngati tipirira, tidzachitanso ufumu ndi Iye: ngati timkana Iye, Iyeyunso adzatikana ife: ngati tikhala osakhulupirika, Iyeyu akhala wokhulupirika; pakuti sakhoza kudzikana yekha. Uwakumbutse izi, ndi kuwachitira umboni pamaso pa Ambuye, kuti asachite makani ndi mau osapindulitsa kanthu, koma ogwetsa iwo akumva. Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nao bwino mau a choonadi. Koma pewa nkhani zopanda pake; pakuti adzapitirira kutsata chisapembedzo, ndipo mau ao adzanyeka chilonda; a iwo ali Himeneo ndi Fileto; ndiwo amene adasokera kunena za choonadi, ponena kuti kuuka kwa akufa kwachitika kale, napasula chikhulupiriro cha ena. Koma ndithu maziko a Mulungu aimika pokhazikika, ndi kukhala nacho chizindikiro ichi, Ambuye azindikira iwo amene ali ake; ndipo, Adzipatule kwa chosalungama yense wakutchula dzina la Ambuye. Koma m'nyumba yaikulu simuli zotengera za golide ndi siliva zokha, komatunso za mtengo ndi dothi; ndipo zina zaulemu, koma zina zopanda ulemu. Ngati tsono munthu adziyeretsa yekha pa izi, adzakhala chotengera cha kuulemu, chipatulidwa, choyenera kuchita nacho Mbuye, chokonzera ntchito yonse yabwino. Koma thawa zilakolako za unyamata, nutsate chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, mtendere, pamodzi ndi iwo akuitana pa Ambuye ndi mitima yoyera. Koma mafunso opusa ndi opanda malango upewe, podziwa kuti abala ndeu. Ndipo kapolo wa Ambuye sayenera kuchita ndeu, komatu akhale woyenera, waulere pa onse, wodziwa kuphunzitsa, woleza, wolangiza iwo akutsutsana mofatsa; ngati kapena Mulungu awapatse iwo chitembenuziro, kukazindikira choonadi, ndipo akadzipulumutse kumsampha wa mdierekezi, m'mene anagwidwa naye, kuchifuniro chake. Koma zindikira ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthawi zowawitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudierekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu; akukhala nao maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; kwa iwonso udzipatule. Pakuti mwa iwo akhala akukwawira m'nyumba, nagwira akazi opusa, osenza akatundu a zoipa zao, otengedwa nazo zilakolako za mitundumitundu: ophunzira nthawi zonse, koma sakhoza konse kufikira kuchizindikiritso cha choonadi. Ndipo monga momwe Yane ndi Yambere anatsutsana naye Mose, kotero iwonso atsutsana nacho choonadi; ndiwo anthu ovunditsitsa mtima, osatsimikizidwa pachikhulupiriro. Koma sadzapitirirapo; pakuti kupusa kwao kudzaonekeratu kwa onse, monganso kupusa kwa iwo aja. Koma iwe watsatatsata chiphunzitso changa, mayendedwe, chitsimikizo mtima, chikhulupiriro, kuleza mtima, chikondi, chipiriro, mazunzo, kumva zowawa; zotere zonga anandichitira m'Antiokeya, m'Ikonio, m'Listara, mazunzo otere onga ndawamva; ndipo m'zonsezi Ambuye anandilanditsa. Ndipo onse akufuna kukhala opembedza m'moyo mwa Khristu Yesu, adzamva mazunzo. Koma anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa. Koma ukhalebe iwe mu izi zimene waziphunzira, nutsimikizika mtima nazo, podziwa amene adakuphunzitsa; ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziwa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu. Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m'chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino. Ndikuchitira umboni pamaso pa Mulungu ndi Khristu Yesu, amene adzaweruza amoyo ndi akufa, ndi pa maonekedwe ake ndi ufumu wake; lalikira mau; chita nao pa nthawi yake, popanda nthawi yake; tsutsa, dzudzula, chenjeza, ndi kuleza mtima konse ndi chiphunzitso. Pakuti idzafika nthawi imene sadzalola chiphunzitso cholamitsa; komatu poyabwa m'khutu adzadziunjikitsa aphunzitsi monga mwa zilakolako za iwo okha: ndipo adzalubza dala pachoonadi, nadzapatukira kutsata nthano zachabe. Koma iwe, khala maso m'zonse, imva zowawa, chita ntchito ya mlaliki wa Uthenga Wabwino, kwaniritsa utumiki wako. Pakuti ndilimkuthiridwa nsembe tsopano, ndipo nthawi ya kumasuka kwanga yafika. Ndalimbana nako kulimbana kwabwino, ndatsiriza njirayo, ndasunga chikhulupiriro: chotsalira wandiikira ine korona wa chilungamo, amene Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa ine tsiku lijalo: ndipo si kwa ine ndekha, komatunso kwa onse amene anakonda maonekedwe ake. Tayesetsa kudza kwa ine msanga: pakuti Dema wandisiya ine, atakonda dziko lino lapansi, napita ku Tesalonika; Kresike ku Galatiya, Tito ku Dalamatiya. Luka yekha ali pamodzi ndi ine. Umtenge Marko, adze pamodzi ndi iwe; pakuti ayenera kunditumikira. Koma Tikiko ndamtuma ku Efeso. Chofunda chija ndinachisiya ku Troasi kwa Karpo, udze nacho pakudza iwe, ndi mabuku, makamaka zikopa zija zolembedwa. Aleksandro wosula mkuwa anandichitira zoipa zambiri: adzambwezera iye Ambuye monga mwa ntchito zake; ameneyo iwenso uchenjere naye; pakuti anatsutsana nao mau athu. Pa chodzikanira changa choyamba panalibe mmodzi anandithangata, koma onse anandisiya; chimenecho chisawerengedwe chowatsutsa. Koma Ambuye anaima nane nandipatsa mphamvu; kuti mwa ine chilalikiro chimveke konsekonse, ndi amitundu onse amve; ndipo ndinalanditsidwa m'kamwa mwa mkango. Ambuye adzandilanditsa ku ntchito yonse yoipa, nadzandipulumutsa ine kulowa Ufumu wake wa Kumwamba; kwa Iye ukhale ulemerero kunthawi za nthawi. Amen. Pereka moni kwa Prisika ndi Akwila, ndi banja la Onesifore. Erasto anakhalira m'Korinto; koma Trofimo ndamsiya wodwala ku Mileto. Tayesetsa kudza isanadze nyengo yachisanu. Akukupatsa moni Yubulo, ndi Pude, ndi Lino, ndi Klaudia, ndi abale onse. Ambuye akhale ndi mzimu wako. Chisomo chikhale nanu. Paulo, kapolo wa Mulungu, ndi mtumwi wa Yesu Khristu, monga mwa chikhulupiriro cha osankhika a Mulungu, ndi chizindikiritso cha choonadi chili monga mwa chipembedzo, m'chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu, wosanamayo, analonjeza zisanayambe nthawi zosayamba; koma pa nyengo za Iye yekha anaonetsa mau ake muulalikiro, umene anandisungitsa ine, monga mwa lamulo la Mpulumutsi wathu Mulungu: kwa Tito, mwana wanga weniweni monga mwa chikhulupiriro cha ife tonse: Chisomo ndi mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Mpulumutsi wathu. Chifukwa cha ichi ndinakusiya iwe m'Krete, kuti ukalongosole zosowa, nukaike akulu m'midzi yonse, monga ndinakulamulira; ngati wina ali wopanda chilema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wokhala nao ana okhulupirira, wosasakaza zake, kapena wosakana kumvera mau. Pakuti woyang'anira ayenera kukhala wopanda chilema, ngati mdindo wa Mulungu; wosati waliuma, wosapsa mtima msanga, wosati wachiwawa, wopanda ndeu, wosati wa chisiriro chonyansa; komatu wokonda kuchereza alendo, wokonda zokoma, wodziweruza, wolungama, woyera mtima, wodziletsa; wogwira mau okhulupirika monga mwa chiphunzitso, kuti akakhoze kuchenjeza m'chiphunzitso cholamitsa, ndi kutsutsa otsutsana naye. Pakuti alipo ambiri osamvera mau, olankhula zopanda pake, ndi onyenga, makamaka iwo akumdulidwe, amene ayenera kutsekedwa pakamwa; ndiwo amene apasula mabanja banja lonse, ndi kuphunzitsa zosayenera chifukwa cha chisiriro chonyansa. Wina wa mwa iwo, ndiye mneneri wa iwo okha, anati, Akrete ndiwo amabodza masiku onse, zilombo zoipa, aumbombo, aulesi. Umboni uwu uli woona. Mwa ichi uwadzudzule mokalipa, kuti akakhale olama m'chikhulupiriro, osasamala nthano zachabe za Chiyuda, ndi malamulo a anthu opatuka kusiyana nacho choonadi. Zonse ziyera kwa iwo amene ayera mtima; koma kwa iwo odetsedwa ndi osakhulupirira kulibe kanthu koyera; komatu zadetsedwa nzeru zao ndi chikumbu mtima chao. Avomereza kuti adziwa Mulungu, koma ndi ntchito zao amkana Iye, popeza ali onyansitsa, ndi osamvera, ndi pa ntchito zonse zabwino osatsimikizidwa. Koma iwe, lankhula zimene ziyenera chiphunzitso cholamitsa: okalamba akhale odzisunga, olemekezeka, odziletsa, olama m'chikhulupiriro, m'chikondi, m'chipiriro. Momwemonso akazi okalamba akhale nao makhalidwe oyenera anthu oyera, osadierekeza, osakodwa nacho chikondi cha pavinyo, akuphunzitsa zokoma; kuti akalangize akazi aang'ono akonde amuna ao, akonde ana ao, akhale odziletsa, odekha, ochita m'nyumba mwao, okoma, akumvera amuna a iwo okha, kuti mau a Mulungu angachitidwe mwano. Momwemonso anyamata uwadandaulire akhale odziletsa; m'zonse udzionetsere wekha chitsanzo cha ntchito zabwino; m'chiphunzitso chako uonetsere chosavunda, ulemekezeko, mau olama osatsutsika; kuti iye wakutsutsana achite manyazi, posakhala nako kanthu koipa kakutinenera ife. Akapolo amvere ambuye ao a iwo okha, nawakondweretse m'zonse; osakana mau ao; osatapa pa zao, komatu aonetsere chikhulupiriko chonse chabwino; kuti akakometsere chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu Mulungu m'zinthu zonse. Pakuti chaonekera chisomo cha Mulungu chakupulumutsa anthu onse, ndi kutiphunzitsa ife kuti, pokana chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, tikhale ndi moyo m'dziko lino odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza; akulindira chiyembekezo chodala, ndi maonekedwe a ulemerero wa Mulungu wamkulu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu; amene anadzipereka yekha m'malo mwa ife, kuti akatiombole ife kuzoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pa ntchito zokoma. Izi lankhula, ndipo uchenjeze, nudzudzule ndi ulamuliro wonse. Munthu asakupeputse. Uwakumbutse iwo agonje kwa akulu, ndi aulamuliro, akhale omvera, okonzeka pa ntchito iliyonse yabwino; asachitire mwano munthu aliyense, asakhale andeu, akhale aulere, naonetsere chifatso chonse pa anthu onse. Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundumitundu, okhala m'dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzake. Koma pamene kukoma mtima, ndi chikondi cha pa anthu, cha Mpulumutsi wathu Mulungu zidanoneka, zosati zochokera m'ntchito za m'chilungamo, zimene tidazichita ife, komatu monga mwa chifundo chake anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera, amene anatsanulira pa ife mochulukira, mwa Yesu Khristu Mpulumutsi wathu; kuti poyesedwa olungama ndi chisomo cha Iyetu, tikayesedwe olowa nyumba monga mwa chiyembekezo cha moyo wosatha. Okhulupirika mauwa, ndipo za izi ndifuna kuti ulimbitse mau, kuti iwo akukhulupirira Mulungu asamalire akhalebe atsogoleri a ntchito zabwino. Izi nzokoma ndi zopindulitsa anthu; koma pewa mafunso opusa, ndi mawerengedwe a mibadwo, ndi ndeu, ndi makani a pamalamulo; pakuti sizipindulitsa, ndipo zili zachabe. Munthu wopatukira chikhulupiriro, utamchenjeza kamodzi ndi kawiri, umkanize, podziwa kuti wotereyo wasandulika konse, nachimwa, nakhala wodzitsutsa yekha. Pamene ndikatuma Aritema kwa iwe, kapena Tikiko, chita changu kudza kwa ine ku Nikopoli: pakuti ndatsimikiza mtima kugonerako nyengo yachisanu. Zena nkhoswe ya milandu, ndi Apolo ufulumire kuwakonzera zaulendo, kuti asasowe kanthu, Ndipo anthu athu aphunzirenso asunge ntchito zabwino zofunika, kuti asakhale osabala zipatso. Akukupatsa moni onse akukhala pamodzi ndi ine. Pereka moni kwa otikondawo m'chikhulupiriro. Chisomo chikhale ndi inu nonse. Paulo, wandende wa Khristu Yesu, ndi Timoteo mbaleyo, kwa Filemoni wokondedwayo ndi wantchito mnzathu, ndi kwa Afiya mlongoyo, ndi Arkipo msilikali mnzathu, ndi kwa Mpingo uli m'nyumba yako: Chisomo kwa inu ndi mtendere za kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu. Ndiyamika Mulungu wanga nthawi zonse, ndi kukumbukira iwe m'mapemphero anga, pakumva za chikondi chako ndi chikhulupiriro uli nacho chakulinga kwa Ambuye Yesu, ndi kwa oyera mtima onse; kuti chiyanjano cha chikhulupiriro chako chikakhale champhamvu podziwa chabwino chilichonse chili mwa inu, cha kwa Khristu. Pakuti ndinali nacho chimwemwe chambiri ndi chisangalatso pa chikondi chako, popeza mitima ya oyera mtima yatsitsimuka mwa iwe, mbale. Momwemo, ndingakhale ndili nako kulimbika mtima kwakukulu m'Khristu kukulamulira chimene chiyenera, koma makamaka ndidandaulira mwa chikondi, pokhala wotere, Paulo nkhalamba, ndipo tsopano wandendenso wa Khristu Yesu; ndikudandaulira chifukwa cha mwana wanga, amene ndambala m'ndende, Onesimo, amene kale sanakupindulira, koma tsopano watipindulira bwino iwe ndi ine; amene ndi yemweyo ndakubwezera iwe, ndiye mtima weniweni wa ine. Ameneyo ndikadafuna ine kumsunga akhale nane, kuti m'malo mwako akadanditumikira ine m'ndende za Uthenga Wabwino: koma wopanda kudziwa mtima wako sindinafuna kuchita kanthu; kuti ubwino wako usakhale monga mokakamiza, komatu mwaufulu. Pakuti kapena anasiyanitsidwa ndi iwe kanthawi chifukwa cha ichi, ndi kuti udzakhala naye nthawi zonse; osatinso monga kapolo, koma woposa kapolo, mbale wokondedwa, makamaka ndi ine, koma koposa nanga ndi iwe, m'thupi, ndiponso mwa Ambuye. Ngati tsono undiyesa woyanjana nawe, umlandire iye monga ine mwini. Koma ngati anakulakwira kanthu, kapena wokongola kanthu, kanthu, kapena wakongola kanthu, undiwerengere ine kameneko; ine Paulo ndichilemba ndi dzanja langa, ndidzachibwezera ine; kuti ndisanene nawe kuti iwe ndiwe mangawa anga. Inde, mbale, ndikondwere nawe mwa Ambuye: utsitsimutse mtima wanga mwa Khristu. Pokhulupirira kumvera kwako ndikulembera iwe, podziwa kuti udzachitanso koposa chimene ndinena. Koma undikonzerenso pogona; pakuti ndiyembekeza kuti mwa mapemphero anu ndidzapatsidwa kwa inu. Epafra wandende mnzanga mwa Khristu Yesu akukupatsa moni; ateronso, Marko, Aristariko, Dema, Luka, antchito anzanga. Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale pamodzi ndi mzimu wanu. Amen. Kale Mulungu analankhula ndi makolo mwa aneneri m'manenedwe ambiri ndi mosiyanasiyana, koma pakutha pake pa masiku ano analankhula ndi ife ndi Mwana amene anamuika wolowa nyumba wa zonse, mwa Iyenso analenga maiko ndi am'mwamba omwe; ameneyo, pokhala ali chinyezimiro cha ulemerero wake, ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake, nanyamula zonse ndi mau a mphamvu yake, m'mene adachita chiyeretso cha zoipa, anakhala pa dzanja lamanja la Ukulu m'Mwamba, atakhala wakuposa angelo, monga momwe adalowa dzina lakuposa iwo. Pakuti kwa mngelo uti anati nthawi iliyonse, Iwe ndiwe Mwana wanga, lero Ine ndakubala Iwe? Ndiponso, Ine ndidzakhala kwa Iye Atate, ndipo Iye adzakhala kwa Ine Mwana? Ndipo pamene atenganso wobadwa woyamba kulowa naye m'dziko, anena, Ndipo amgwadire Iye angelo onse a Mulungu. Ndipo za angelo anenadi, Amene ayesa angelo ake mizimu, ndi omtumikira Iye akhale malawi amoto. Koma ponena za Mwana, ati, Mpando wachifumu wanu, Mulungu, ufikira nthawi za nthawi; ndipo ndodo yachifumu yoongoka ndiyo ndodo ya ufumu wanu. Mwakonda chilungamo, ndi kudana nacho choipa; mwa ichi Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wakudzozani ndi mafuta a chikondwerero chenicheni koposa anzanu. Ndipo, Inu, Ambuye, pachiyambipo munaika maziko ake a dziko, ndipo miyamba ili ntchito ya manja anu. Iyo idzataika; komatu mukhalitsa; ndipo iyo yonse idzasuka monga malaya; ndi monga chofunda mudzaipinda monga malaya, ndipo idzasanduka; koma Inu ndinu yemweyo, ndipo zaka zanu sizidzatha. Koma za mngelo uti anati nthawi iliyonse, Khala pa dzanja lamanja langa, Kufikira ndikaika adani ako mpando wa kumapazi ako? Kodi siili yonse mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzalowa chipulumutso? Mwa ichi tiyenera kusamaliradi zimene tidazimvazi kuti kapena tingatengedwe ndi kusiyana nazo. Pakuti ngati mau adalankhulidwa ndi angelo adakhala okhazikika, ndipo cholakwira chilichonse ndi chosamvera chalandira mphotho yobwezera yolungama, tidzapulumuka bwanji ife, tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotero? Chimene Ambuye adayamba kuchilankhula, ndipo iwo adachimva anatilimbikitsira ife; pochita umboni pamodzi nao Mulungunso ndi zizindikiro, ndi zozizwitsa ndi mphamvu za mitundumitundu ndi zogawira za Mzimu Woyera, monga mwa chifuniro chake. Pakuti sanagonjetsera angelo dziko lilinkudza limene tinenali. Koma wina anachita umboni pena, nati, Munthu nchiyani kuti mumkumbukira iye? Kapena mwana wa munthu kuti mucheza naye? Munamchepsa pang'ono ndi angelo, mudamveka iye korona wa ulemerero ndi ulemu, ndipo mudamuika iye woyang'anira ntchito za manja anu; mudagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake. Pakuti muja adagonjetsa zonse kwa iye, sanasiyapo kanthu kosamgonjera iye. Koma sitinayamba tsopano apa kuona zonse zimgonjera. Koma timpenya Iye amene adamchepsa pang'ono ndi angelo, ndiye Yesu, chifukwa cha zowawa za imfa, wovala korona wa ulemerero ndi ulemu, kuti ndi chisomo cha Mulungu alawe imfa m'malo mwa munthu aliyense. Pakuti kunamuyenera Iye amene zonse zili chifukwa cha Iye, ndi zonse mwa Iye, pakutenga ana ambiri alowe ulemerero, kumkonza wamphumphu mtsogoleri woyamba wa chipulumutso chao mwa zowawa. Pakuti Iye wakuyeretsa ndi iwo akuyeretsedwa achokera onse mwa mmodzi; chifukwa cha ichi alibe manyazi kuwatcha iwo abale. Ndi kuti, Ndidzalalikira dzina lanu kwa abale anga, pakati pa Mpingo ndidzakuimbirani. Ndiponso, Ndidzamtama Iye. Ndiponso, Taonani, Ine ndi ana amene Mulungu anandipatsa. Popeza tsono ana ndiwo a mwazi ndi nyama, Iyenso momwemo adalawa nao makhalidwe omwewo kuti mwa imfa akamuononge iye amene anali nayo mphamvu ya imfa, ndiye mdierekezi; nakamasule iwo onse amene, chifukwa cha kuopa imfa, m'moyo wao wonse adamangidwa ukapolo. Pakuti ndithu salandira angelo, koma alandira mbeu ya Abrahamu. Potero kudamuyenera kufanizidwa ndi abale m'zonse, kuti akadzakhala mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika m'zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke dipo la zoipa za anthu. Pakuti popeza adamva zowawa, poyesedwa yekha, akhoza kuthandiza iwo amene ayesedwa. Potero, abale oyera mtima, olandirana nao maitanidwe akumwamba, lingirirani za Mtumwi ndi Mkulu wa ansembe wa chivomerezo chathu, Yesu; amene anakhala wokhulupirika kwa Iye adamuikayo, monganso Mose m'nyumba yake yonse. Pakuti ameneyo wayesedwa woyenera ulemerero woposa Mose, monga momwe iye amene anaimanga nyumba ali nao ulemerero woposa nyumbayi. Pakuti nyumba iliyonse ili naye wina woimanga; koma wozimanga zonse ndiye Mulungu. Ndipo Mosetu anali wokhulupirika m'nyumba yake yonse, monga mnyamata, achitire umboni izi zidzalankhulidwazi; koma Khristu monga mwana, wosunga nyumba yake; ndife nyumba yake, ngati tigwiritsa kulimbika mtima ndi kudzitamandira kwa chiyembekezocho, kuchigwira kufikira chitsiriziro. Momwemo, monga anena Mzimu Woyera, Lero ngati mudzamva mau ake, musaumitse mitima yanu, monga m'kupsetsa mtimamo, monga muja tsiku la chiyesero m'chipululu, chimene makolo anu anandiyesa nacho, ndi kundivomereza, naona ntchito zanga zaka makumi anai. Momwemo ndinakwiya nao mbadwo uwu, ndipo ndinati, Nthawi zonse amasochera mumtima; koma sanazindikira njira zanga iwowa; Monga ndinalumbira m'ukali wanga: Ngati adzalowa mpumulo wanga! Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupirira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo; komatu dandaulirananani nokha tsiku ndi tsiku, pamene patchedwa, Lero; kuti angaumitsidwe wina wa inu ndi chenjerero la uchimo; pakuti takhala ife olandirana ndi Khristu, ngatitu tigwiritsa chiyambi cha kutama kwathu kuchigwira kufikira chitsiriziro; umo anenamo, Lero ngati mudzamva mau ake, musaumitse mitima yanu, monga pa kupsetsa mtima. Pakuti ndi ayani, pakumva, anapsetsa mtima? Kodi si onse aja adatuluka m'Ejipito ndi Mose? Koma anakwiya ndi ayani zaka makumi anai? Kodi si ndi awo adachimwawo, amene matupi ao adagwa m'chipululu? Ndipo adawalumbirira ayani kuti asalowe mpumulo wake? Si awo kodi osamverawo? Ndipo tiona kuti sanakhoza kulowa chifukwa cha kusakhulupirira. Chifukwa chake tiope kuti kapena likatsala lonjezano lakulowa mpumulo wake, wina wa inu angaoneke ngati adaliperewera. Pakuti kwa ifenso walalikidwa Uthenga Wabwino, monganso kwa iwo; koma iwowa sanapindula nao mau omvekawo, popeza sanasanganizika ndi chikhulupiriro mwa iwo amene adawamva. Popeza ife amene takhulupirira tilowa mpumulowo, monga momwe ananena, Monga ndalumbira mu mkwiyo wanga, ngati adzalowa mpumulo wanga. Zingakhale ntchitozo zidatsirizika kuyambira kuzika kwa dziko lapansi. Pakuti wanena pena za tsiku lachisanu ndi chiwiri, natero, Ndipo Mulungu anapumula tsiku lachisanu ndi chiwiri, kuleka ntchito zake zonse. Ndipo m'menemonso, Ngati adzalowa mpumulo wanga. Popeza tsono patsala kuti ena akalowa momwemo, ndi iwo amene Uthenga Wabwino unalalikidwa kwa iwo kale sanalowamo chifukwa cha kusamvera, alangizanso tsiku lina, ndi kunena m'Davide, itapita nthawi yaikulu yakuti, Lero, monga kwanenedwa kale, Lero ngati mudzamva mau ake, musaumitse mitima yanu. Pakuti ngati Yoswa akadawapumitsa iwo, sakadalankhula m'tsogolomo za tsiku lina. Momwemo utsalira mpumulo wa Sabata wa kwa anthu a Mulungu. Pakuti iye amene adalowa mpumulo wake, adapumulanso mwini wake kuntchito zake, monganso Mulungu kuzake za Iye. Chifukwa chake tichite changu cha kulowa mpumulowo, kuti wina angagwe m'chitsanzo chomwe cha kusamvera. Pakuti mau a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m'mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima. Ndipo palibe cholembedwa chosaonekera pamaso pake, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye. Popeza tsono tili naye Mkulu wa ansembe wamkulu, wopyoza miyamba, Yesu mwana wa Mulungu, tigwiritsitse chivomerezo chathu. Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo. Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa. Pakuti mkulu wa ansembe aliyense, wotengedwa mwa anthu, amaikika chifukwa cha anthu m'zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke mitulo, ndiponso nsembe chifukwa cha machimo: akhale wokhoza kumva chifundo ndi osadziwa ndi olakwa, popeza iye yekhanso amazingwa ndi chifooko; ndipo chifukwa chakecho ayenera, monga m'malo a anthuwo, moteronso m'malo a iye yekha, kupereka nsembe chifukwa cha machimo. Ndipo palibe munthu adzitengera ulemuwo mwini wake, komatu iye amene aitanidwa ndi Mulungu, monga momwenso Aroni. Koteronso Khristu sanadzilemekeza yekha ayesedwe Mkulu wa ansembe, komatu Iye amene analankhula kwa Iye, Mwana wanga ndi Iwe, lero Ine ndakubala Iwe. Monga anenanso mwina, Iwe ndiwe wansembe wa nthawi zonse monga mwa dongosolo la Melkizedeki. Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu, angakhale anali Mwana, anaphunzira kumvera ndi izi adamva kuwawa nazo; ndipo pamene anakonzeka wamphumphu anakhala kwa onse akumvera Iye chifukwa cha chipulumutso chosatha; wotchedwa ndi Mulungu mkulu wa ansembe monga mwa dongosolo la Melkizedeki. Za iye tili nao mau ambiri kuwanena, ndi otilaka powatanthauzira, popeza mwagontha m'makutu. Pakuti mungakhale mwayenera kukhala aphunzitsi chifukwa cha nyengoyi, muli nako kusowanso kuti wina aphunzitse inu zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu; ndipo mukhala onga ofuna mkaka, osati chakudya chotafuna. Pakuti yense wakudya mkaka alibe chizolowezi cha mau a chilungamo; pakuti ali khanda. Koma chakudya chotafuna chili cha anthu akulu misinkhu, amene mwa kuchita nazo anazoloweretsa zizindikiritso zao kusiyanitsa chabwino ndi choipa. Mwa ichi, polekana nao mau a chiyambidwe cha Khristu, tipitirire kutsata ukulu msinkhu; osaikanso maziko a kutembenuka mtima kusiyana nazo ntchito zakufa, ndi a chikhulupiriro cha pa Mulungu, a chiphunzitso cha ubatizo, a kuika manja, a kuuka kwa akufa, ndi a chiweruziro chosatha. Ndipo ichi tidzachita, akatilola Mulungu. Pakuti sikutheka kuwakonzanso, atembenuke mtima, iwo amene anaunikidwa pa nthawi yake, nalawa mphatso ya Kumwamba, nakhala olandirana naye Mzimu Woyera, nalawa mau okoma a Mulungu, ndi mphamvu ya nthawi ilinkudza, koma anagwa m'chisokero; popeza adzipachikiranso okha Mwana wa Mulungu, namchititsa manyazi poyera. Pakuti nthaka imene idamwa mvula iigwera kawirikawiri, nipatsa therere loyenera iwo amene adailimira, ilandira dalitso lochokera kwa Mulungu: koma ikabala minga ndi mitungwi, itayika; nitsala pang'ono ikadatembereredwa; chitsiriziro chake ndicho kutenthedwa. Koma, okondedwa, takopeka mtima kuti za inu zili zoposa ndi zophatikana chipulumutso, tingakhale titero pakulankhula; pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe. Koma tikhumba kuti yense wa inu aonetsere changu chomwechi cholinga kuchiyembekezo chokwanira kufikira chitsiriziro; kuti musakhale aulesi, koma akuwatsanza iwo amene alikulowa malonjezano mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima. Pakuti pamene Mulungu analonjezana naye Abrahamu, popeza analibe wamkulu woposa kumlumbira, analumbira pa Iye yekha, nati, Kudalitsatu ndidzakudalitsa iwe, ndipo kuchulukitsa ndidzakuchulukitsa iwe. Ndipo potero atapirira analandira lonjezanolo. Pakuti anthu amalumbira pa wamkulu; ndipo m'chitsutsano chao chilichonse lumbiro litsiriza kutsimikiza. Momwemo Mulungu, pofuna kuonetsera mochulukira kwa olowa a lonjezano kuti chifuniro chake sichisinthika, analowa pakati ndi lumbiro; kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, m'mene Mulungu sakhoza kunama, tikakhale nacho chotichenjeza cholimba, ife amene tidathawira kuchigwira chiyembekezo choikika pamaso pathu; chimene tili nacho ngati nangula wa moyo, chokhazikika ndi cholimbanso, ndi chakulowa m'katikati mwa chophimba; m'mene Yesu mtsogoleri analowamo chifukwa cha ife, atakhala mkulu wa ansembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo la Melkizedeki. Pakuti Melkizedeki uyu, mfumu ya Salemu, wansembe wa Mulungu Wamkulukulu, amene anakomana ndi Abrahamu, pobwera iye adawapha mafumu aja, namdalitsa, amenenso Abrahamu anamgawira limodzi la magawo khumi la zonse (ndiye posandulika, poyamba ali mfumu ya chilungamo, pameneponso mfumu ya Salemu, ndiko, mfumu ya mtendere; wopanda atate wake, wopanda amake, wopanda mawerengedwe a chibadwidwe chake, alibe chiyambi cha masiku ake kapena chitsiriziro cha moyo wake, wofanizidwa ndi Mwana wa Mulungu), iyeyu wakhala wansembe kosalekeza. Koma tapenyani ukulu wake wa iyeyu, amene Abrahamu, kholo lalikulu, anampatsa limodzi la magawo khumi la zosankhika za kunkhondo. Ndipo iwotu mwa ana a Levi akulandira ntchito yakupereka nsembe, ali nalo lamulo lakuti atenge limodzi la magawo khumi kwa anthu monga mwa chilamulo, ndiko kwa abale ao, angakhale adatuluka m'chuuno cha Abrahamu; koma iye amene mawerengedwe a chibadwidwe chake sachokera mwa iwo, anatenga limodzi la magawo khumi kwa Abrahamu, namdalitsa iye amene ali nao malonjezano. Ndipo popanda chitsutsano konse wamng'ono adalitsidwa ndi wamkulu. Ndipo pano anthu ofeka alandira limodzi la magawo khumi; koma apo iye, woti adamchitira umboni kuti ali ndi moyo. Ndipo kuli ngati kunena, mwa Abrahamu Levinso wakulandira limodzilimodzi la magawo khumi adapereka limodzi la magawo khumi; pakuti pajapo anali m'chuuno cha atate wake, pamene Melkizedeki anakomana naye. Ndipo pakadakhala ungwiro mwa unsembe wa Chilevi (pakuti momwemo anthu analandira chilamulo), pakadatsala kusowa kotani kuti auke wansembe wina monga mwa dongosolo la Melkizedeki, wosayesedwa monga mwa dongosolo la Aroni? Pakuti posandulika unsembe, kufunikanso kuti lamulo lisandulike. Pakuti Iye amene izi zineneka za Iye, akhala wa fuko lina, wa ili palibe munthu watumikira guwa la nsembe. Pakuti kwadziwikadi kuti Ambuye wathu anatuluka mwa Yuda; za fuko ili Mose sanalankhula kanthu ka ansembe. Ndipo kwadziwikatu koposa ndithu, ngati auka wansembe wina monga mwa mafanidwe a Melkizedeki, amene wakhala si monga mwa lamulo la lamuliro la kwa thupi, komatu monga mwa mphamvu ya moyo wosaonongeka; pakuti amchitira umboni, Iwe ndiwe wansembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo la Melkizedeki. Pakutitu kuli kutaya kwake kwa lamulo lidadza kalelo, chifukwa cha kufooka kwake, ndi kusapindulitsa kwake, (pakuti chilamulo sichinachitira kanthu kakhale kopanda chilema), ndipo kulinso kulowa nacho chiyembekezo choposa, chimene tiyandikira nacho kwa Mulungu. Ndipo monga momwe sikudachitika kopanda lumbiro; (pakuti iwotu anayesedwa ansembe kopanda lumbiro; koma Iye ndi lumbiro mwa Iye amene anenana kwa Iye, Walumbira Ambuye ndipo sadzalapa, iwe ndiwe wansembe nthawi yosatha). Momwemonso Yesu wakhala Nkhoswe ya pangano loposa. Ndipo iwo ndiwo ambiri anakhala ansembe, popeza imfa idawaletsa asakhalebe; koma Iye chifukwa kuti akhala Iye nthawi yosatha ali nao unsembe wosasinthika, kuchokera komweko akhoza kupulumutsa konsekonse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye, popeza ali nao moyo wake chikhalire wa kuwapembedzera iwo. Pakuti mkulu wa ansembe wotere anatiyenera ife, woyera mtima, wopanda choipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ochimwa, wakukhala wopitirira miyamba; amene alibe chifukwa cha kupereka nsembe tsiku ndi tsiku monga akulu a ansembe, yoyambira chifukwa cha zoipa za iwo eni, yinayi chifukwa cha zoipa za anthu; pakuti ichi anachita kamodzi, kwatha, podzipereka yekha. Pakuti chilamulo chimaika akulu a ansembe anthu, okhala nacho chifooko; koma mau a lumbirolo, amene anafika chitapita chilamulo, aika Mwana, woyesedwa wopanda chilema kunthawi zonse. Koma mutu wa izi tanenazi ndi uwu: Tili naye Mkulu wa ansembe wotere, amene anakhala pa dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Ukulu m'Kumwamba, Mtumiki wa malo opatulika, ndi wa chihema choona, chimene Ambuye anachimanga, si munthu ai. Pakuti mkulu wa ansembe aliyense aikidwa kupereka mitulo, ndiponso nsembe; potero nkufunika kuti ameneyo akhale nako kanthunso kakupereka. Ndipo Iye akadakhala padziko, sakadakhala konse wansembe, popeza pali iwo akupereka mitulo monga mwa lamulo; amene atumikira chifaniziro ndi mthunzi wa zakumwambazo monga Mose achenjezedwa m'mene anafuna kupanga chihema: pakuti, Chenjera, ati, uchite zonse monga mwa chitsanzocho chaonetsedwa kwa iwe m'phiri. Koma tsopano Iye walandira chitumikiro chomveka koposa, umonso ali Nkhoswe ya pangano labwino loposa, limene likhazikika pa malonjezano oposa. Pakuti loyamba lija likadakhala lopanda chilema sakadafuna malo a lachiwirilo. Pakuti powatchulira iwo chifukwa, anena, Taonani, akudza masiku, anena Ambuye, Ndipo ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya Israele, ndi nyumba ya Yuda, losati longa pangano ndinalichita ndi makolo ao, tsikuli ndinawagwira kudzanja iwo kuwatsogolera atuluke m'dziko la Ejipito; kuti iwo sanakhalabe m'pangano langa, ndipo Ine sindinawasamalira iwo, anena Ambuye. Pakuti ili ndi pangano ndidzalipangana ndi nyumba ya Israele, atapita masiku ajawa, anena Ambuye: Ndidzapatsa malamulo anga kuwalonga m'nzeru zao, ndipo pamtima pao ndidzawalemba iwo; ndipo ndidzawakhalira iwo Mulungu, ndipo iwo adzandikhalira Ine anthu: Ndipo sadzaphunzitsa yense mfulu mnzake, ndipo yense mbale wake, ndi kuti, Zindikira Ambuye: Pakuti onse adzadziwa Ine, kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu wa iwo. Kuti ndidzachitira chifundo zosalungama zao, ndipo zoipa zao sindidzazikumbukanso. Pakunena Iye, Latsopano, anagugitsa loyambali. Koma chimene chilinkuguga ndi kusukuluka, chayandikira kukanganuka. Ndipo chingakhale chipangano choyambachi chinali nazo zoikika za kulambira, ndi malo opatulika a pa dziko lapansi. Pakuti chihema chidakonzeka, choyamba chija, m'menemo munali choikapo nyali, ndi gome, ndi mkate woonekera; paja paitanidwa Malo Opatulika. Koma m'kati mwa chophimba chachiwiri, chihema chonenedwa Malo Opatulika kwambiri; okhala nayo mbale ya zofukiza yagolide ndi likasa la chipangano, lokuta ponsepo ndi golide, momwemo munali mbiya yagolide yosungamo mana, ndi ndodo ya Aroni idaphukayo, ndi magome a chipangano; ndi pamwamba pake akerubi a ulemerero akuchititsa mthunzi pachotetezerapo; za izi sitikhoza kunena tsopano paderapadera. Ndipo izi zitakonzeka kotero, ansembe amalowa m'chihema choyamba kosalekeza, ndi kutsiriza kulambirako; koma kulowa m'chachiwiri, mkulu wa ansembe yekha kamodzi pachaka, wosati wopanda mwazi, umene apereka chifukwa cha iye yekha, ndi zolakwa za anthu; Mzimu Woyera wodziwitsa nako, kuti njira yolowa nayo kumalo opatulika siinaonetsedwe, pokhala chihema choyamba chili chilili; ndicho chiphiphiritso cha kunthawi yomweyi, m'mene mitulo ndi nsembenso zinaperekedwa zosakhoza, ponena za chikumbu mtima, kuyesa wangwiro wolambirayo. Popeza akhala zoikika za thupi zokha (ndi zakudya, ndi zakumwa, ndi masambidwe osiyanasiyana), oikidwa kufikira nthawi yakukonzanso. Koma atafika Khristu, Mkulu wa ansembe wa zokoma zilinkudza mwa, chihema chachikulu ndi changwiro choposa, chosamangika ndi manja, ndiko kunena kuti, chosati cha chilengedwe ichi, kapena mwa mwazi wa mbuzi ndi anaang'ombe, koma mwa mwazi wa Iye yekha, analowa kamodzi kumalo opatulika, atalandirapo chiombolo chosatha. Pakuti ngati mwazi wa mbuzi ndi ng'ombe zamphongo, ndi makala a ng'ombe yamthandi owazawaza pa iwo odetsedwa, upatutsa kufikira chiyeretso cha thupi; koposa kotani nanga mwazi wa Khristu amene anadzipereka yekha wopanda chilema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa chikumbu mtima chanu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo? Ndipo mwa ichi ali Nkhoswe ya chipangano chatsopano, kotero kuti, popeza kudachitika imfa yakuombola zolakwa za pa chipangano choyamba, oitanidwawo akalandire lonjezano la zolowa zosatha. Pakuti pamene pali chopangiratu pafunika pafike imfa ya wolemberayo. Pakuti chopangiratu chiona mphamvu atafa mwini wake; popeza chilibe mphamvu konse pokhala wolemberayo ali ndi moyo; momwemo choyambachonso sichinakonzeka chopanda mwazi. Pakuti pamene Mose adalankhulira anthu onse lamulo lililonse monga mwa chilamulo, anatenga mwazi wa anaang'ombe ndi mbuzi, pamodzi ndi madzi ndi ubweya wofiira ndi hisope, nawaza buku lomwe, ndi anthu onse, nati, Uwu ndi mwazi wa chipangano Mulungu adakulamulani. Ndiponso chihema ndi zotengera zonse za utumikiro anaziwaza momwemo ndi mwaziwo. Ndipo monga mwa chilamulo zitsala zinthu pang'ono zosayeretsedwa ndi mwazi, ndipo wopanda kukhetsa mwazi palibe kukhululukidwa kwa machimo. Pomwepo padafunika kuti zifaniziro za zinthu za m'Mwamba ziyeretsedwe ndi izi; koma zam'mwamba zenizeni ziyeretsedwe ndi nsembe zoposa izi. Pakuti Khristu sanalowa m'malo opatulika omangika ndi manja, akutsanza oonawo; komatu m'Mwamba momwe, kuonekera tsopano pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife; kosati kuti adzipereke yekha kawirikawiri; monga mkulu wa ansembe alowa m'malo opatulika chaka ndi chaka ndi mwazi wosati wake; chikadatero, kukadamuyenera kumva zowawa kawirikawiri kuyambira kuzika kwa dziko lapansi; koma tsopano kamodzi pa chitsirizo cha nthawizo waonekera kuchotsa uchimo mwa nsembe ya Iye yekha. Ndipo popeza kwaikikatu kwa anthu kufa kamodzi, ndipo atafa, chiweruziro; kotero Khristunso ataperekedwa nsembe kamodzi kukasenza machimo a ambiri, adzaonekera pa nthawi yachiwiri, wopanda uchimo, kwa iwo amene amlindirira, kufikira chipulumutso. Pakuti chilamulo, pokhala nao mthunzi wa zokoma zilinkudza, osati chifaniziro chenicheni cha zinthuzo, sichikhozatu, ndi nsembe zomwezi chaka ndi chaka, zimene azipereka kosalekeza, kuwayesera angwiro iwo akuyandikira. Pakadapanda kutero, kodi sakadaleka kuzipereka, chifukwa otumikirawo sakadakhala nacho chikumbu mtima cha machimo, popeza adayeretsedwa kamodzi? Komatu mu izizo muli chikumbukiro cha machimo chaka ndi chaka. Pakuti sikutheka kuti mwazi wa ng'ombe zamphongo, ndi mbuzi ukachotsera machimo. Mwa ichi polowa m'dziko lapansi, anena, Nsembe ndi chopereka simunazifuna, koma thupi munandikonzera Ine. Nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa machimo simunakondwera nazo; pamenepo ndinati, Taonani, ndafika, (Pamutu pake pa buku palembedwa za Ine) kudzachita chifuniro chanu, Mulungu. Pakunena pamwamba apa, kuti, Nsembe ndi zopereka ndi nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa machimo simunazifuna, kapena kukondwera nazo (zimene ziperekedwa monga mwa lamulo), pamenepo anati, Taonani, ndafika kudzachita chifuniro chanu. Achotsa choyambacho, kuti akaike chachiwiricho. Ndi chifuniro chimenecho tayeretsedwa mwa chopereka cha thupi la Yesu Khristu, kamodzi, kwatha. Ndipotu wansembe aliyense amaima tsiku ndi tsiku, natumikira, napereka nsembe zomwezi kawirikawiri, zimene sizikhoza konse kuchotsa machimo; koma Iye, m'mene adapereka nsembe imodzi chifukwa cha machimo, anakhala pa dzanja lamanja la Mulungu chikhalire; kuyambira pomwepo alindirira, kufikira adani ake aikidwa akhale mpando kumapazi ake. Pakuti ndi chipereko chimodzi anawayesera angwiro chikhalire iwo oyeretsedwa. Koma Mzimu Woyeranso atichitira umboni; pakuti adatha kunena, Ichi ndi chipangano ndidzapangana nao, atapita masiku ajawo, anena Ambuye: Ndidzapereka malamulo anga akhale pamtima pao; ndipo pa nzeru zao ndidzawalemba; ndipo machimo ao ndi masaweruziko ao sindidzawakumbukiranso. Koma pomwe pali chikhululukiro cha machimo palibenso chopereka cha kwa uchimo. Ndipo pokhala nacho, abale, chilimbikitso chakulowa m'malo opatulika, ndi mwazi wa Yesu, pa njira yatsopano ndi yamoyo, imene adatikonzera, mwa chotchinga, ndicho thupi lake; ndipo popeza tili naye wansembe wamkulu wosunga nyumba ya Mulungu; tiyandikire ndi mtima woona, m'chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbu mtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera; tigwiritse chivomerezo chosagwedera cha chiyembekezo chathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika; ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika. Pakuti tikachimwa ife eni ake, titatha kulandira chidziwitso cha choonadi, siitsalanso nsembe ya kwa machimo, koma kulindira kwina koopsa kwa chiweruziro, ndi kutentha kwake kwa moto wakuononga otsutsana nao. Munthu wopeputsa chilamulo cha Mose angofa opanda chifundo pa mboni ziwiri kapena zitatu: ndipo mutani, kulanga koposa kotani nanga adzayesedwa woyenera iye amene anapondereza Mwana wa Mulungu, nayesa mwazi wa chipangano umene anayeretsedwa nao chinthu wamba, nachitira chipongwe Mzimu wa chisomo; pakuti timdziwa Iye amene anati, Kubwezera chilango nkwanga, Ine ndidzabwezera. Ndiponso, Ambuye adzaweruza anthu ake. Kugwa m'manja a Mulungu wamoyo nkoopsa. Koma tadzikumbutsani masiku akale, m'menemo mutaunikidwa mudapirira chitsutsano chachikulu cha zowawa; pena pochitidwa chinthu chooneredwa mwa matonzo ndi zisautso; penanso polawana nao iwo ochitidwa zotere. Pakuti munamva chifundo ndi iwo a m'ndende, ndiponso mudalola mokondwera kulandidwa kwa chuma chanu, pozindikira kuti muli nacho nokha chuma choposa chachikhalire. Potero musataye kulimbika kwanu, kumene kuli nacho chobwezera mphotho chachikulu. Pakuti chikusowani chipiriro, kuti pamene mwachita chifuniro cha Mulungu, mukalandire lonjezano. Pakuti katsala kanthawi kakang'onong'ono, ndipo wakudzayo adzafika, wosachedwa. Koma wolungama wangayo adzakhala ndi moyo wochokera m'chikhulupiriro: Ndipo ngati abwerera, moyo wanga ulibe kukondwera mwa iye. Koma ife si ndife a iwo akubwerera kulowa chitayiko; koma a iwo a chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo. Koma chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka. Pakuti momwemo akulu anachitidwa umboni. Ndi chikhulupiriro tizindikira kuti maiko ndi a m'mwamba omwe anakonzedwa ndi mau a Mulungu, kotero kuti zinthu zopenyeka sizinapangidwa zochokera mwa zoonekazo. Ndi chikhulupiriro Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa ija ya Kaini, imene anachitidwa umboni nayo kuti anali wolungama; nachitapo umboni Mulungu pa mitulo yake; ndipo momwemo iye, angakhale adafa alankhulabe. Ndi chikhulupiriro Enoki anatengedwa kuti angaone imfa; ndipo sanapezeka, popeza Mulungu adamtenga: pakuti asanamtenge, anachitidwa umboni kuti anakondweretsa Mulungu; koma wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye. Ndi chikhulupiriro Nowa, pochenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zisanapenyeke, ndi pochita mantha, anamanga chingalawa cha kupulumutsiramo iwo a m'nyumba yake; kumene anatsutsa nako dziko lapansi, nakhala wolowa nyumba wa chilungamo chili monga mwa chikhulupiriro. Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poitanidwa, anamvera kutuluka kunka kumalo amene adzalandira ngati cholowa; ndipo anatuluka wosadziwa kumene akamukako. Ndi chikhulupiriro anakhala mlendo kudziko la lonjezano, losati lake, nakhalira m'mahema pamodzi ndi Isaki ndi Yakobo, olowa nyumba pamodzi ndi iye a lonjezano lomwelo; pakuti analindirira mudzi wokhala nao maziko, mmisiri wake ndi womanga wake ndiye Mulungu. Ndi chikhulupiriro Sara yemwe analandira mphamvu yakukhala ndi pakati, patapita nthawi yake, popeza anamwerengera wokhulupirika Iye amene adalonjeza; mwa ichinso kudachokera kwa mmodzi, ndiye ngati wakufa, aunyinji ngati nyenyezi za m'mwamba, ndi ngati mchenga, uli m'mphepete mwa nyanja, osawerengeka. Iwo onse adamwalira m'chikhulupiriro, osalandira malonjezano, komatu adawaona ndi kuwalankhula kutali, navomereza kuti ali alendo ndi ogonera padziko. Pakuti iwo akunena zotere aonetserapo kuti alikufuna dziko likhale lao. Ndipotu akadakumbukira lijalo adatulukamo akadaona njira yakubwera nayo. Koma tsopano akhumba lina loposa, ndilo la m'Mwamba; mwa ichi Mulungu sachita manyazi nao poitanidwa Mulungu wao; pakuti adawakonzera mudzi. Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poyesedwa, anapereka nsembe Isaki, ndipo iye mene adalandira malonjezano anapereka mwana wake wayekha; amene kudanenedwa za iye, kuti, Mwa Isaki mbeu yako idzaitanidwa: poyesera iye kuti Mulungu ngwokhoza kuukitsa, ngakhale kwa akufa; kuchokera komwe, pachiphiphiritso, anamlandiranso. Ndi chikhulupiriro Isaki anadalitsa Yakobo ndi Esau, zingakhale za zinthu zilinkudza. Ndi chikhulupiriro Yakobo, poti alinkufa, anadalitsa yense wa ana a Yosefe; napembedza potsamira pa mutu wa ndodo yake. Ndi chikhulupiriro, Yosefe, pakumwalira, anatchula za matulukidwe a ana a Israele; nalamula za mafupa ake. Ndi chikhulupiriro Mose, pobadwa, anabisidwa miyezi itatu ndi akum'bala, popeza anaona kuti ali mwana wokongola; ndipo sanaopa chilamuliro cha mfumu. Ndi chikhulupiriro Mose, atakula msinkhu, anakana kutchedwa mwana wake wa mwana wamkazi wa Farao; nasankhula kuchitidwa zoipa pamodzi ndi anthu a Mulungu, kosati kukhala nazo zokondweretsa za zoipa nthawi; nawerenga tonzo la Khristu chuma choposa zolemera za Aejipito; pakuti anapenyerera chobwezera cha mphotho. Ndi chikhulupiriro anasiya Ejipito, wosaopa mkwiyo wa mfumu; pakuti anapirira molimbika, monga ngati kuona wosaonekayo. Ndi chikhulupiriro anachita Paska, ndi kuwaza kwa mwazi, kuti wakuononga ana oyamba angawakhudze iwo. Ndi chikhulupiriro anaoloka Nyanja Yofiira kupita ngati pamtunda: ndiko Aejipito poyesanso anamizidwa. Ndi chikhulupiriro malinga a Yeriko adagwa atazunguliridwa masiku asanu ndi awiri. Ndi chikhulupiriro Rahabu wadama uja sanaonongeka pamodzi ndi osamverawo, popeza analandira ozonda ndi mtendere. Ndipo ndinene chiyaninso? Pakuti idzandiperewera nthawi ndifotokozere za Gideoni, Baraki, Samisoni, Yefita; za Davide, ndi Samuele ndi aneneri; mene mwa chikhulupiriro anagonjetsa maufumu, anachita chilungamo, analandira malonjezano, anatseka pakamwa mikango, nazima mphamvu ya moto, napulumuka lupanga lakuthwa, analimbikitsidwa pokhala ofooka, anakula mphamvu kunkhondo, anapirikitsa magulu a nkhondo yachilendo. Akazi analandira akufa ao mwa kuuka kwa akufa; ndipo ena anakwapulidwa, osalola kuomboledwa, kuti akalandire kuuka koposa; koma ena anayesedwa ndi matonzo ndi zokwapulira, ndiponso nsinga, ndi kuwatsekera m'ndende; anaponyedwa miyala, anachekedwa pakati, anayesedwa, anaphedwa ndi lupanga, anayendayenda ovala zikopa zankhosa, ndi zikopa zambuzi, nakhala osowa, osautsidwa, ochitidwa zoipa, (amenewo dziko lapansi silinayenera iwo), osokerera m'mapululu, ndi m'mapiri, ndi m'mapanga, ndi m'mauna a dziko. Ndipo iwo onse adachitidwa umboni mwa chikhulupiriro, sanalandira lonjezanolo, popeza Mulungu adatikonzera ife kanthu koposa, kuti iwo asayesedwe amphumphu opanda ife. Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nao mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu, Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala pa dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu. Pakuti talingirirani Iye amene adapirira ndi ochimwa otsutsana naye kotere, kuti mungaleme ndi kukomoka m'moyo mwanu. Simunakana kufikira mwazi pogwirana nalo tchimo; ndipo mwaiwala dandauliro limene linena nanu monga ndi ana, Mwana wanga, usayese chopepuka kulanga kwa Ambuye, kapena usakomoke podzudzulidwa ndi Iye; pakuti iye amene Ambuye amkonda amlanga, nakwapula mwana aliyense amlandira. Mukapirira kufikira kulangidwa Mulungu achitira inu monga ngati ana; pakuti mwana wanji amene atate wake wosamlanga? Koma ngati mukhala opanda chilango, chimene onse adalawako, pamenepo muli am'thengo, si ana ai. Komanso, tinali nao atate a thupi lathu akutilanga, ndipo tinawalemekeza; kodi sitidzagonjera Atate wa mizimu koposa nanga, ndi kukhala ndi moyo? Pakutitu iwo anatilanga masiku owerengeka monga kudawakomera; koma Iye atero, kukatipindulitsa, kuti tikalandirane nao pa chiyero chake. Chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondwetsa, komatu chowawa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo. Mwa ichi limbitsani manja ogooka, ndi maondo olobodoka; ndipo lambulani miseu yolunjika yoyendamo mapazi anu, kuti chotsimphinacho chisapatulidwe m'njira, koma chichiritsidwe. Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye: ndi kuyang'anira kuti pangakhale wina wakuperewera chisomo cha Mulungu, kuti ungapuke muzu wina wa kuwawa mtima ungavute inu, ndipo aunyinji angadetsedwe nao; kuti pangakhale wachigololo, kapena wamnyozo, ngati Esau, amene anagulitsa ukulu wake wobadwa nao mtanda umodzi wa chakudya. Pakuti mudziwa kutinso pamene anafuna kulowa dalitsolo, anakanidwa (pakuti sanapeza malo akulapa), angakhale analifunafuna ndi misozi. Pakuti simunayandikira phiri lokhudzika, ndi lakupsa moto, ndi pakuda bii, ndi mdima, ndi namondwe, ndi mau a lipenga, ndi manenedwe a mau, manenedwe amene iwo adamvawo anapempha kuti asawaonjezerepo mau; pakuti sanakhoza kulola cholamulidwacho. Ingakhale nyama ikakhudza phirilo, idzaponyedwa miyala; ndipo maonekedwewo anali oopsa otere, kuti Mose anati, Ndiopatu ndi kunthunthumira. Komatu mwayandikira kuphiri la Ziyoni, ndi mudzi wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wa Kumwamba, ndi kwa unyinji wochuluka wa angelo, ndi kwa msonkhano wa onse ndi Mpingo wa obadwa oyamba olembedwa m'Mwamba, ndi kwa Mulungu Woweruza wa onse, ndi kwa mizimu ya olungama oyesedwa angwiro, ndi kwa Yesu Nkhoswe ya chipangano chatsopano, ndi kwa mwazi wa kuwaza wakulankhula chokoma choposa mwazi wa Abele. Penyani musakane wolankhulayo. Pakuti ngati iwowa sanapulumuka, pomkana Iye amene anawachenjeza padziko, koposatu sitidzapulumuka ife, odzipatulira kwa Iye wa Kumwamba; amene mau ake anagwedeza dziko pamenepo; koma tsopano adalonjeza, ndi kuti, Kamodzinso ndidzagwedeza, si dziko lokha, komanso m'mwamba. Ndipo ichi, chakuti kamodzinso, chilozera kusuntha kwake kwa zinthu zogwedezeka, monga kwa zinthu zolengedwa, kuti zinthu zosagwedezeka zikhale. Mwa ichi polandira ufumu wosagwedezeka, tikhale nacho chisomo, chimene tikatumikire nacho Mulungu momkondweretsa, ndi kumchitira ulemu ndi mantha. Pakuti Mulungu wathu ndiye moto wonyeketsa. Chikondi cha pa abale chikhalebe. Musaiwale kuchereza alendo; pakuti mwa ichi ena anachereza angelo osachidziwa. Kumbukirani am'nsinga, monga am'nsinga anzao; ochitidwa zoipa, monga ngati inunso adatero nanu m'thupi. Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu. Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu. Kotero kuti tinena molimbika mtima, Mthandizi wanga ndiye Ambuye; sindidzaopa; adzandichitira chiyani munthu? Kumbukirani atsogoleri anu, amene analankhula nanu Mau a Mulungu; ndipo poyang'anira chitsiriziro cha mayendedwe ao mutsanze chikhulupiriro chao. Yesu Khristu ali yemweyo dzulo, ndi lero, ndi kunthawi zonse. Musatengedwe ndi maphunzitso a mitundumitundu, ndi achilendo; pakuti nkokoma kuti mtima ukhazikike ndi chisomo; kosati ndi zakudya, zimene iwo adazitsata sanapindula nazo. Tili nalo guwa la nsembe, limene iwo akutumikira chihema alibe ulamuliro wa kudyako. Pakuti matupi a nyama zija, mwazi wa izo umatengedwa, ndi mkulu wa ansembe kulowa m'malo opatulidwa, chifukwa cha zoipa, amatenthedwa kunja kwa tsasa. Mwa ichi Yesunso, kuti akayeretse anthuwo mwa mwazi wa Iye yekha, adamva chowawa kunja kwa chipata. Chifukwa chake titulukire kwa Iye kunja kwa tsasa osenza tonzo lake. Pakuti pano tilibe mudzi wokhalitsa, komatu tifunafuna ulinkudzawo. Potero mwa Iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake. Koma musaiwale kuchitira chokoma ndi kugawira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo. Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuwerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu. Mutipempherere ife; pakuti takopeka mtima kuti tili nacho chikumbu mtima chokoma m'zonse, pofuna kukhala nao makhalidwe abwino. Ndipo ndikudandaulirani koposa kuchita ichi, kuti kubwera kwanga kwa inu kufulumidwe. Koma Mulungu wa mtendere amene anabwera naye wotuluka mwa akufa Mbusa wamkulu wa nkhosa ndi mwazi wa chipangano chosatha, ndiye Ambuye wathu Yesu, akuyeseni inu opanda chilema m'chinthu chilichonse chabwino, kuti muchite chifuniro chake; ndi kuchita mwa ife chomkondweretsa pamaso pake, mwa Yesu Khristu; kwa Iyeyu ukhale ulemerero kunthawi za nthawi. Amen. Koma ndidandaulira inu, abale, lolani mau a chidandauliro; pakutinso ndalembera inu mwachidule. Zindikirani kuti mbale wathu Timoteo wamasulidwa; pamodzi ndi iye, ngati akudza msanga, ndidzakuonani inu. Perekani moni kwa atsogoleri anu onse, ndi oyera mtima onse. Akupatsani moni iwo a ku Italiya. Chisomo chikhale ndi inu nonse, Amen. Yakobo, kapolo wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu, kwa mafuko khumi ndi awiri a m'chibalaliko: ndikupatsani moni. Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, m'mene mukugwa m'mayesero a mitundumitundu; pozindikira kuti chiyesedwe cha chikhulupiriro chanu chichita chipiriro. Koma chipiriro chikhale nayo ntchito yake yangwiro, kuti mukakhale angwiro ndi opanda chilema, osasowa kanthu konse. Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye. Koma apemphe ndi chikhulupiriro, wosakayika konse; pakuti wokayikayo afanana ndi funde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuwinduka nayo. Pakuti asayese munthu uyu kuti adzalandira kanthu kwa Ambuye; munthu wa mitima iwiri akhala wosinkhasinkha pa njira zake zonse. Koma mbale woluluka adzitamandire pa ukulu wake; pakuti adzapita monga duwa la udzu. Pakuti latuluka dzuwa ndi kutentha kwake, ndipo laumitsa udzu; ndipo lathothoka duwa lake, ndi ukoma wa maonekedwe ake waonongeka; koteronso wachuma adzafota m'mayendedwe ake. Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda Iye. Munthu poyesedwa, asanena, Ndiyesedwa ndi Mulungu; pakuti Mulungu sakhoza kuyesedwa ndi zoipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu: koma munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera, nichimnyenga. Pamenepo chilakolakocho chitaima, chibala uchimo; ndipo uchimo, utakula msinkhu, ubala imfa. Musanyengedwe, abale anga okondedwa. Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro. Mwa chifuniro chake mwini anatibala ife ndi mau a choonadi, kuti tikhale ife ngati zipatso zoundukula za zolengedwa zake. Mudziwa, abale anga okondedwa, kuti munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima. Pakuti mkwiyo wa munthu suchita chilungamo cha Mulungu. Mwa ichi, mutavula chinyanso chonse ndi chisefukiro cha choipa, landirani ndi chifatso mau ookedwa mwa inu, okhoza kupulumutsa moyo wanu. Khalani akuchita mau, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha. Pakuti ngati munthu ali wakumva mau, wosati wakuchita, iyeyu afanana ndi munthu wakuyang'anira nkhope yake ya chibadwidwe chake m'kalirole; pakuti wadziyang'anira yekha, nachoka, naiwala pompaja nali wotani. Koma iye wakupenyerera m'lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero chipenyerere, ameneyo, posakhala wakumva wakuiwala, komatu wakuchita ntchito, adzakhala wodala m'kuchita kwake. Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthuyu nkopanda pake. Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m'chisautso chao, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi. Abale anga, pakuti muli nacho chikhulupiriro cha Ambuye wathu Yesu Khristu, Ambuye wa ulemerero, musakhale okondera ndi kusamala maonekedwe. Pakuti akalowa m'sunagoge mwanu munthu wovala mphete yagolide, ndi chovala chokometsetsa, ndipo akalowanso munthu wosauka ndi chovala chodetsa; ndipo mukapenyerera iye wovala chokometsetsa, nimukati naye, Inu mukhale apa pabwino; ndipo mukati kwa wosaukayo, Iwe, imauko, kapena, khala pansi pa mpando wa mapazi anga; kodi simunasiyanitsa mwa inu nokha, ndi kukhala oweruza oganizira zoipa? Mverani, abale anga okondedwa; kodi Mulungu sanasankha osauka a dziko lapansi akhale olemera ndi chikhulupiriro, ndi olowa nyumba a ufumu umene adaulonjeza kwa iwo akumkonda Iye? Koma inu mumanyoza munthu wosauka. Kodi sakusautsani inu achuma, nakukokerani iwowa kumabwalo a milandu? Kodi sachitira mwano iwowa dzina lokomali muitanidwa nalo? Koma ngati muchita chikwanirire lamulolo lachifumu, monga mwa malembo, Uzikonda mnzako monga udzikonda wekha, muchita bwino: koma ngati musamala maonekedwe, muchita uchimo, ndipo mutsutsidwa ndi chilamulo monga olakwa. Pakuti amene aliyense angasunge malamulo onse, koma akakhumudwa pa limodzi, iyeyu wachimwira onse. Pakuti Iye wakuti, Usachite chigololo, anatinso, Usaphe. Ndipo ukapanda kuchita chigololo, koma ukapha, wakhala wolakwira lamulo. Lankhulani motero, ndipo chitani motero, monga anthu amene adzaweruzidwa ndi lamulo la ufulu. Pakuti chiweruziro chilibe chifundo kwa iye amene sanachita chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro. Chipindulo chake nchiyani, abale anga, munthu akanena, Ndili nacho chikhulupiriro, koma alibe ntchito? Kodi chikhulupirirocho chikhoza kumpulumutsa? Mbale kapena mlongo akakhala wausiwa, nichikamsowa chakudya cha tsiku lake, ndipo wina wa inu akanena nao, Mukani ndi mtendere, mukafunde ndi kukhuta; osawapatsa iwo zosowa za pathupi; kupindula kwake nchiyani? Momwemonso chikhulupiriro, chikapanda kukhala nacho ntchito, chikhala chakufa m'kati mwakemo. Koma wina akati, Iwe uli nacho chikhulupiriro, ndipo ine ndili nazo ntchito; undionetse ine chikhulupiriro chako chopanda ntchito zako, ndipo ine ndidzakuonetsa iwe chikhulupiriro changa chotuluka m'ntchito zanga. Ukhulupirira iwe kuti Mulungu ali mmodzi; uchita bwino; ziwanda zikhulupiriranso, ndipo zinthunthumira. Koma ufuna kuzindikira kodi, munthu wopanda pake iwe, kuti chikhulupiriro chopanda ntchito chili chabe? Abrahamu kholo lathu, sanayesedwa wolungama ndi ntchito kodi, paja adapereka mwana wake Isaki nsembe pa guwa la nsembe? Upenya kuti chikhulupiriro chidachita pamodzi ndi ntchito zake, ndipo motuluka mwa ntchito chikhulupiriro chidayesedwa changwiro; ndipo anakwaniridwa malembo onenawa, Ndipo Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kudawerengedwa kwa iye chilungamo; ndipo anatchedwa bwenzi la Mulungu. Mupenya kuti munthu ayesedwa wolungama ndi ntchito yake, osati ndi chikhulupiriro chokha. Ndipo momwemonso sanayesedwa wolungama Rahabu mkazi wa damayo ndi ntchito kodi, popeza adalandira amithenga, nawatulutsa adzere njira ina? Pakuti monga thupi lopanda mzimu lili lakufa, koteronso chikhulupiriro chopanda ntchito chili chakufa. Musakhale aphunzitsi ambiri, abale anga, podziwa kuti tidzalangika koposa. Pakuti timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri. Munthu akapanda kukhumudwa pa mau, iye ndiye munthu wangwiro, wokhoza kumanganso thupi lonse. Koma ngati tiikira akavalo zogwirira m'kamwa mwao atimvere, tipotolozanso thupi lao lonse. Taonani, zombonso, zingakhale zazikulu zotere, nizitengedwa ndi mphepo zolimba, zipotozeka ndi tsigiro laling'ono ndithu kumene kulikonse afuna wogwira tsigiro. Kotero lilimenso lili chiwalo chaching'ono, ndipo lidzikuzira zazikulu. Taonani, kamoto kakang'ono kayatsa nkhuni zambiri! Ndipo lilime ndilo moto; ngati dziko la chosalungama mwa ziwalo zathu laikika lilime, ndili lodetsa thupi lonse, niliyatsa mayendedwe a chibadwidwe, ndipo liyatsidwa ndi Gehena. Pakuti mtundu uliwonse wa nyama ndi wa mbalamenso, wa zokwawa, ndi wa zam'nyanja, zimazoloweretsedwa, ndipo zazoloweretsedwa ndi anthu; koma lilime palibe munthu akhoza kulizoloweretsa; lili choipa chotakataka, lodzala ndi ululu wakupha. Timayamika Ambuye ndi Atate nalo; nalonso timatemberera anthu, okhala monga mwa mafanizidwe a Mulungu; Mochokera m'kamwa momwemo mutuluka chiyamiko ndi temberero. Abale anga, izi siziyenera kutero. Kodi kasupe atulutsira pa uno womwewo madzi okoma ndi owawa? Kodi mkuyu ukhoza kubala azitona, abale anga, kapena mpesa kubala nkhuyu? Kotero madzi amchere sakhoza kutulutsa okoma. Ndani ali wanzeru, ndi waluso mwa inu? Aonetsere ndi mayendedwe ake abwino ntchito zake mu nzeru yofatsa. Koma mukakhala nako kaduka kowawa, ndi chotetana m'mtima mwanu, musadzitamandira, ndipo musamanama potsutsana nacho choonadi. Nzeru iyi, sindiyo yotsika kumwamba, komatu ili ya padziko, ya chifuniro cha chibadwidwe, ya ziwanda. Pakuti pomwe pali kaduka ndi zotetana, pamenepo pali chisokonekero ndi chochita choipa chilichonse. Koma nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, yosadzikometsera pamaso. Ndipo chipatso cha chilungamo chifesedwa mumtendere kwa iwo akuchita mtendere. Zichokera kuti nkhondo, zichokera kuti zolimbana mwa inu? Kodi sizichokera kuzikhumbitso zanu zochita nkhondo m'ziwalo zanu? Mulakalaka, ndipo zikusowani; mukupha, nimuchita kaduka, ndipo simukhoza kupeza; mulimbana, nimuchita nkhondo; mulibe kanthu, chifukwa simupempha. Mupempha, ndipo simulandira, popeza mupempha koipa, kuti mukachimwaze pochita zikhumbitso zanu. Akazi achigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu. Kodi muyesa kapena kuti malembo angonena chabe? Kodi Mzimuyo adamkhalitsa mwa ife akhumbitsa kuchita nsanje? Koma apatsa chisomo choposa. Potero anena malembo, Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo odzichepetsa. Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani inu. Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu. Sambani m'manja, ochimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iwiri inu. Khalani osautsidwa, lirani, lirani misozi; kuseka kwanu kusanduke kulira, ndi chimwemwe chanu chisanduke chisoni. Dzichepetseni pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani. Musamanenerana, abale. Wonenera mbale, kapena woweruza mbale wake, anenera lamulo, naweruza lamulo: koma ngati uweruza lamulo, suli wochita lamulo, komatu woweruza. Woika lamulo ndi woweruza ndiye mmodzi, ndiye amene akhoza kupulumutsa ndi kuononga; koma iwe woweruza mnzako ndiwe yani? Nanga tsono, inu akunena, Lero kapena mawa tidzapita kulowa kumudzi wakutiwakuti, ndipo tidzagonerako ndi kutsatsa malonda, ndi kupindula nao; inu amene simudziwa chimene chidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka. Mukadanena inu, Akalola Mulungu, ndipo tikakhala ndi moyo, tidzachita kakutikakuti. Koma tsopano mudzitamandira m'kudzikuza kwanu; kudzitamandira kulikonse kotero nkoipa. Potero kwa iye amene adziwa kuchita bwino, ndipo sachita, kwa iye kuli tchimo. Nanga tsono achuma inu, lirani ndi kuchema chifukwa cha masautso anu akudza pa inu. Chuma chanu chaola ndi zovala zanu zajiwa ndi njenjete. Golide wanu ndi siliva wanu zachita dzimbiri, ndipo dzimbiri lake lidzachita mboni zoneneza inu, ndipo zidzadya nyama yanu ngati moto. Mwadzikundikira chuma masiku otsiriza. Taonani, mphotho ya antchitowo anasenga m'minda yanu, yosungidwa ndi inu powanyenga, ifuula; ndipo mafuulo a osengawo adalowa m'makutu a Ambuye wa makamu. Mwadyerera padziko, ndipo mwachita zokukondweretsani; mwadyetsa mitima yanu m'tsiku lakupha. Munamtsutsa, munapha wolungamayo, iye sakaniza inu. Potero, lezani mtima, abale, kufikira kudza kwake kwa Ambuye. Taonani, wolima munda alindira chipatso chofunikatu cha dziko, ndi kuleza mtima nacho kufikira chikalandira mvula ya chizimalupsa ndi masika. Lezani mtima inunso, limbitsani mitima yanu; pakuti kudza kwake kwa Ambuye kuyandikira. Musaipidwe wina ndi mnzake, abale, kuti mungaweruzidwe. Taonani, woweruza aima pakhomo. Tengani, abale, chitsanzo cha kumva zowawa ndi kuleza mtima, aneneri amene analankhula m'dzina la Ambuye. Taonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo. Koma makamaka, abale anga, musalumbire, kungakhale kutchula kumwamba kapena dziko, kapena lumbiro lina lililonse; koma inde wanu akhale inde, ndi iai wanu akhale iai; kuti mungagwe m'chiweruziro. Kodi wina wa inu akumva zowawa? Apemphere. Kodi wina asekera? Aimbire. Pali wina kodi adwala mwa inu? Adziitanire akulu a Mpingo, ndipo apemphere pa iye, atamdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye: ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Ambuye adzamuukitsa; ndipo ngati adachita machimo adzakhululukidwa kwa iye. Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake. Eliya anali munthu wakumva zomwezi tizimva ife, ndipo anapemphera chipempherere kuti isavumbe mvula; ndipo siinagwa mvula pa dziko zaka zitatu kudza miyezi isanu ndi umodzi. Ndipo anapempheranso; ndipo m'mwamba munatsika mvula, ndi dziko lidabala zipatso zake. Abale anga, ngati wina wa inu asochera posiyana ndi choonadi, ndipo ambweza iye mnzake; azindikire, kuti iye amene abweza wochimwa kunjira yake yosochera adzapulumutsa munthu kwa imfa, ndipo adzavundikira machimo aunyinji. Petro, mtumwi wa Yesu Khristu, kwa osankhidwa akukhala alendo a chibalaliko a ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asiya, ndi Bitiniya, monga mwa kudziwiratu kwa Mulungu Atate, m'chiyeretso cha Mzimu, chochitira chimvero, ndi kuwaza kwa mwazi wa Yesu Khristu: Chisomo, ndi mtendere zichulukire inu. Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu; kuti tilandire cholowa chosavunda ndi chosadetsa ndi chosafota, chosungikira m'Mwamba inu, amene musungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mwa chikhulupiriro, kufikira chipulumutso chokonzeka kukavumbulutsidwa nthawi yotsiriza. M'menemo mukondwera, kungakhale tsopano kanthawi, ngati kuyenera, mukachitidwe chisoni ndi mayesero a mitundumitundu, kuti mayesedwe a chikhulupiriro chanu, ndiwo a mtengo wake woposa wa golide amene angotayika, ngakhale ayesedwa ndi moto, akapezedwe ochitira chiyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa vumbulutso la Yesu Khristu; amene mungakhale simunamuona mumkonda; amene mungakhale simumpenya tsopano, pokhulupirira, mukondwera naye ndi chimwemwe chosaneneka, ndi cha ulemerero: ndi kulandira chitsiriziro cha chikhulupiriro chanu, ndicho chipulumutso cha moyo wanu. Kunena za chipulumutso ichi anafunafuna nasanthula aneneri, pakunenera za chisomo chikudzerani; ndi kusanthula nthawi yiti, kapena nthawi yanji Mzimu wa Khristu wokhala mwa iwo analozera, pakuchitiratu umboni wa masautso a Khristu, ndi ulemerero wotsatana nao. Kwa iwo amene kudavumbulutsidwa, kuti sanadzitumikira iwo okha, koma inu, ndi zinthu izi, zimene zauzidwa kwa inu tsopano, mwa iwo amene anakulalikirani Uthenga Wabwino mwa Mzimu Woyera, wotumidwa kuchokera Kumwamba; zinthu izi angelo alakalaka kusuzumiramo. Mwa ichi, podzimanga m'chuuno, kunena za mtima wanu, mukhale odzisunga, nimuyembekeze konsekonse chisomo chilikutengedwa kudza nacho kwa inu m'vumbulutso la Yesu Khristu; monga ana omvera osadzifanizitsanso ndi zilakolako zakale, pokhala osadziwa inu; komatu monga Iye wakuitana inu ali woyera mtima, khalani inunso oyera mtima m'makhalidwe anu onse; popeza kwalembedwa, Muzikhala oyera mtima, pakuti Ine ndine woyera mtima. Ndipo mukamuitana ngati Atate, Iye amene aweruza monga mwa ntchito ya yense, wopanda tsankho, khalani ndi mantha nthawi ya chilendo chanu; podziwa kuti simunaomboledwa ndi zovunda, golide ndi siliva, kusiyana nao makhalidwe anu achabe ochokera kwa makolo anu: koma ndi mwazi wa mtengo wake wapatali monga wa mwanawankhosa wopanda chilema, ndi wopanda banga, ndiwo mwazi wa Khristu: amene anazindikirikatu lisanakhazikike dziko lapansi, koma anaonetsedwa pa chitsiriziro cha nthawi, chifukwa cha inu amene mwa Iye mukhulupirira Mulungu wakumuukitsa Iye kwa akufa, ndi kumpatsa Iye ulemerero; kotero kuti chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu chikhale pa Mulungu. Popeza mwayeretsa moyo wanu pakumvera choonadi kuti mukakonde abale ndi chikondi chosanyenga, mukondane kwenikweni kuchokera kumtima; inu amene mudabadwanso, osati ndi mbeu yofeka, komatu yosaola, mwa mau a Mulungu amoyo ndi okhalitsa. Popeza, Anthu onse akunga udzu, ndi ulemerero wao wonse ngati duwa la udzu. Udzuwo ungofota, ndi duwa lake lingogwa; koma Mau a Mulungu akhala chikhalire. Ndipo mau olalikidwa kwa inu ndi awo. Momwemo pakutaya choipa chonse, ndi chinyengo chonse, ndi maonekedwe onyenga, ndi kaduka, ndi masinjiriro onse, lirani monga makanda alero mkaka woyenera, wopanda chinyengo, kuti mukakule nao kufikira chipulumutso; ngati mwalawa kuti Ambuye ali wokoma mtima; amene pakudza kwa Iye, mwala wamoyo, wokanidwatu ndi anthu, koma ndi Mulungu wosankhika, waulemu, inunso ngati miyala yamoyo mumangidwa nyumba ya uzimu, kuti mukhale ansembe oyera mtima, akupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa Yesu Khristu. Chifukwa kwalembedwa m'lembo, Taona, ndiika m'Ziyoni mwala wotsiriza wa pangodya, wosankhika, wa mtengo wake; ndipo wokhulupirira Iye sadzanyazitsidwa. Kwa inu tsono akukhulupirira, ali wa mtengo wake; koma kwa iwo osakhulupirira, Mwala umene omangawo anaukana, womwewo unayesedwa mutu wa pangodya. Ndipo, Mwala wakukhumudwa nao, ndi thanthwe lophunthwitsa. Kwa iwo akukhumudwa ndi mau, pokhala osamvera, kumenekonso adaikidwako. Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa; inu amene kale simunali anthu, koma tsopano muli anthu a Mulungu; amene kale simunalandira chifundo, koma tsopano mwalandira chifundo. Okondedwa, ndikudandaulirani ngati alendo ndi ogonera mudzikanize zilakolako za thupi zimene zichita nkhondo pa moyo; ndipo mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, m'mene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m'tsiku la kuyang'anira. Tadzigonjani kwa zoikika zonse za anthu, chifukwa cha Ambuye; ngakhale kwa mfumu, monga mutu wa onse; kapena kwa akazembe, monga otumidwa ndi iye kukalanga ochita zoipa, koma kusimba ochita zabwino. Pakuti chifuniro cha Mulungu chitere, kuti ndi kuchita zabwino mukatontholetse chipulukiro cha anthu opusa; monga mfulu, koma osakhala nao ufulu monga chobisira choipa, koma ngati akapolo a Mulungu. Chitirani ulemu anthu onse. Kondani abale. Opani Mulungu, Chitirani mfumu ulemu. Anyamata inu, gonjerani ambuye anu ndi kuopa konse, osati abwino ndi aulere okha, komanso aukali. Pakuti ichi ndi chisomo ngati munthu, chifukwa cha chikumbumtima pa Mulungu alola zachisoni, pakumva zowawa wosaziyenera. Pakuti mbiri yokoma yanji, mukapirira pochimwa ndi kubwanyulidwapo? Komatu, ngati pochita zabwino, ndi kumvako ndiko chisomo pa Mulungu. Pakuti kudzachita ichi mwaitanidwa; pakutinso Khristu anamva zowawa m'malo mwanu, nakusiyirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake; amene sanachita tchimo, ndipo m'kamwa mwake sichinapezedwa chinyengo; amene pochitidwa chipongwe sanabwezera chipongwe, pakumva zowawa, sanaopsa, koma anapereka mlandu kwa Iye woweruza kolungama; amene anasenza machimo athu mwini yekha m'thupi mwake pamtanda, kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo; ameneyo mikwingwirima yake munachiritsidwa nayo. Pakuti munalikusochera ngati nkhosa; koma tsopano mwabwera kwa Mbusa ndi Woyang'anira wa moyo wanu. Momwemonso, akazi inu, mverani amuna anu a inu nokha; kuti, ngatinso ena samvera mau, akakodwe opanda mau mwa mayendedwe a akazi; pakuona mayendedwe anu oyera ndi kuopa kwanu. Amene kukometsera kwanu kusakhale kwa kunja, kuluka tsitsi ndi kuvala za golide, kapena kuvala chovala; koma kukhale munthu wobisika wamtima, m'chovala chosaola cha mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu. Pakuti koteronso kale akazi oyera mtima, akuyembekezera Mulungu, anadzikometsera okha, namvera amuna ao a iwo okha; monga Sara anamvera Abrahamu, namutcha iye mbuye; ameneyo mukhala ana ake ngati muchita bwino, osaopa choopsa chilichonse. Momwemonso amuna inu, khalani nao monga mwa chidziwitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu, monganso wolowa nyumba pamodzi wa chisomo cha moyo, kuti mapemphero anu angaletsedwe. Chotsalira, khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa; osabwezera choipa ndi choipa, kapena chipongwe ndi chipongwe, koma penatu madalitso; pakuti kudzatsata ichi mwaitanidwa, kuti mukalandire dalitso. Pakuti, Iye wofuna kukonda moyo, ndi kuona masiku abwino, aletse lilime lake lisanene choipa, ndi milomo yake isalankhule chinyengo; ndipo apatuke pachoipa, nachite chabwino; afunefune mtendere ndi kuulondola. Pakuti maso a Ambuye ali pa olungama, ndi makutu ake akumva pembedzo lao; koma nkhope ya Ambuye ili pa ochita zoipa. Ndipo ndani iye amene adzakuchitirani choipa, ngati muchita nacho changu chinthu chabwino? Komatu ngatinso mukumva zowawa chifukwa cha chilungamo, odala inu; ndipo musaope pakuwaopa iwo, kapena musadere nkhawa; koma mumpatulikitse Ambuye Khristu m'mitima yanu; okonzeka nthawi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chili mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha; ndi kukhala nacho chikumbu mtima chabwino, kuti umo akunenerani, iwo akunenera konama mayendedwe anu abwino m'Khristu akachitidwe manyazi. Pakuti, kumva zowawa chifukwa cha kuchita zabwino, ndi kumva zowawa chifukwa cha kuchita zoipa, nkwabwino kumva zowawa chifukwa cha kuchita zabwino, ngati chitero chifuniro cha Mulungu. Pakuti Khristunso adamva zowawa kamodzi, chifukwa cha machimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m'thupi, koma wopatsidwa moyo mumzimu; m'menemonso anapita, nalalikira mizimu inali m'ndende, imene inakhala yosamvera kale, pamene kuleza mtima kwa Mulungu kunalindira, m'masiku a Nowa, pokhala m'kukonzeka chingalawa, m'menemo owerengeka, ndiwo amoyo asanu ndi atatu, anapulumutsidwa mwa madzi; chimenenso chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lake la thupi, komatu funso lake la chikumbu mtima chokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Khristu; amene akhala pa dzanja lamanja la Mulungu, atalowa m'Mwamba; pali angelo, ndi maulamuliro, ndi zimphamvu, zonse zimgonjera. Popeza Khristu adamva zowawa m'thupi, mudzikonzere mtima womwewo; pakuti iye amene adamva zowawa m'thupi walekana nalo tchimo; kuti nthawi yotsalira simukakhalenso ndi moyo m'thupi kutsata zilakolako za anthu, koma chifuniro cha Mulungu. Pakuti nthawi yapitayi idatifikira kuchita chifuno cha amitundu, poyendayenda ife m'kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, maimwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka; m'menemo ayesa nchachilendo kuti simuthamanga nao kufikira kusefukira komwe kwa chitayiko, nakuchitirani mwano; amenewo adzamwerengera Iye wokhala wokonzeka kuweruza amoyo ndi akufa. Pakuti chifukwa cha ichi walalikidwa Uthenga Wabwino kwa iwonso adafawo, kuti akaweruzidwe monga mwa anthu m'thupi, koma akakhale ndi moyo monga mwa Mulungu mumzimu. Koma chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi; chifukwa chake khalani anzeru, ndipo dikirani m'mapemphero; koposa zonse mukhale nacho chikondano chenicheni mwa inu nokha; pakuti chikondano chikwiriritsa unyinji wa machimo; mucherezane wina ndi mnzake, osadandaula: monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu; akalankhula wina, alankhule ngati manenedwe a Mulungu; wina akatumikira, achite ngati mu mphamvu imene Mulungu ampatsa, kuti m'zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu, amene ali nao ulemerero ndi mphamvu kunthawi za nthawi. Amen. Okondedwa, musazizwe ndi mayesedwe amoto adakugwerani inu akhale chakukuyesani, ngati chinthu chachilendo chachitika nanu: koma popeza mulawana ndi Khristu zowawa zake, kondwerani: kutinso pa vumbulutso la ulemerero wake mukakondwere kwakukulukulu. Mukatonzedwa pa dzina la Khristu, odala inu; pakuti Mzimu wa ulemerero, ndi Mzimu wa Mulungu apuma pa inu. Pakuti asamve zowawa wina wa inu ngati wambanda, kapena mbala, kapena wochita zoipa, kapena ngati wodudukira; koma akamva zowawa ngati mkhristu asachite manyazi; koma alemekeze Mulungu m'dzina ili. Chifukwa yafika nthawi kuti chiweruziro chiyambe pa nyumba ya Mulungu; koma ngati chiyamba ndi ife, chitsiriziro cha iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu chidzakhala chiyani? Ndipo ngati munthu wolungama apulumuka ndi kuyesetsa kokhakokha, munthu wosapembedza ndi wochimwa adzaoneka kuti? Koteronso iwo akumva zowawa monga mwa chifuniro cha Mulungu aike moyo wao ndi kuchita zokoma m'manja a Wolenga wokhulupirika. Akulu tsono mwa inu ndiwadandaulira, ine mkulu mnzanu ndi mboni ya zowawa za Khristu, ndinenso wolawana nao ulemerero udzavumbulutsikawo: Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang'anira, osati mokakamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu; osati monga ochita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma okhala zitsanzo za gululo. Ndipo pakuonekera Mbusa wamkulu, mudzalandira korona wa ulemerero, wosafota. Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa. Potero dzichepetseni pansi pa dzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthawi yake akakukwezeni; ndi kutaya pa Iye nkhawa yanu yonse, pakuti Iye asamalira inu. Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire: ameneyo mumkanize okhazikika m'chikhulupiriro, podziwa kuti zowawa zomwezo zilimkukwaniridwa pa abale anu ali m'dziko. Ndipo Mulungu wa chisomo chonse, amene adakuitanani kulowa ulemerero wake wosatha mwa Khristu, mutamva zowawa kanthawi, adzafikitsa inu opanda chilema mwini wake, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu. Kwa Iye kukhale mphamvu kunthawi za nthawi. Amen. Mwa Silivano, mbale wathu wokhulupirika monga ndimayesa, ndalembera kwa inu mwachidule, ndi kudandaulira, ndi kuchita umboni, kuti chisomo choona cha Mulungu ndi ichi; m'chimenechi muimemo. Iye wa ku Babiloni wosankhidwa pamodzi nanu akulankhulani; ateronso Marko mwana wanga. Mupatsane moni ndi chipsompsono cha chikondi. Mtendere ukhale ndi inu nonse muli mwa Khristu. Simoni Petro, kapolo ndi mtumwi wa Yesu Khristu kwa iwo amene adalandira chikhulupiriro cha mtengo wake womwewo ndi ife, m'chilungamo cha Mulungu wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu: Chisomo kwa inu ndi mtendere zichulukitsidwe m'chidziwitso cha Mulungu ndi Yesu Ambuye wathu. Popeza mphamvu ya umulungu wake idatipatsa ife zonse za pamoyo ndi chipembedzo, mwa chidziwitso cha Iye amene adatiitana ife ndi ulemerero ndi ukoma wake wa Iye yekha; mwa izi adatipatsa malonjezano a mtengo wake ndi akulu ndithu; kuti mwa izi mukakhale oyanjana nao umulungu wake, mutapulumuka kuchivundi chili pa dziko lapansi m'chilakolako. Ndipo mwa ichi chomwe, pakutengeraponso changu chonse, muonjezerapo ukoma pa chikhulupiriro chanu, ndi paukoma chizindikiritso; ndi pachizindikiritso chodziletsa; ndi pachodziletsa chipiriro; ndi pachipiriro chipembedzo; ndi pachipembedzo chikondi cha pa abale; ndi pachikondi cha pa abale chikondi. Pakuti izi zikakhala ndi inu, ndipo zikachuluka, zidzachita kuti musakhale aulesi kapena opanda zipatso pa chizindikiritso cha Ambuye Yesu Khristu. Pakuti iye wakusowa izi ali wakhungu, wa chimbuuzi, woiwala matsukidwe ake potaya zoipa zake zakale. Momwemo abale, onjezani kuchita changu kukhazikitsa maitanidwe ndi masankhulidwe anu; pakuti mukachita izi, simudzakhumudwa nthawi zonse; pakuti kotero kudzaonjezedwa kwa inu kolemerera khomo lakulowa ufumu wosatha wa Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu. Mwa ichi sindidzaleka kukukumbutsani inu nthawi zonse za izi, mungakhale muzidziwa nimukhazikika m'choonadi chili ndi inu. Ndipo ndichiyesa chokoma, pokhala ine m'msasa uwu, kukutsitsimutsani ndi kukukumbutsani; podziwa kuti kuleka kwa msasa wanga kuli pafupi, monganso Ambuye wathu Yesu Khristu anandilangiza. Koma ndidzachitanso changu kosalekeza kuti nditachoka ine, mudzakhoza kukumbukira izi. Pakuti sitinatsata miyambi yachabe, pamene tinakudziwitsani mphamvu ndi maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Khristu, koma tinapenya m'maso ukulu wake. Pakuti analandira kwa Mulungu Atate ulemu ndi ulemerero, pakumdzera Iye mau otere ochokera ku ulemerero waukulu, Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene Ine ndikondwera naye; ndipo mau awa ochokera Kumwamba tidawamva ife, pokhala pamodzi ndi Iye m'phiri lopatulika lija. Ndipo tili nao mau a chinenero okhazikika koposa; amene muchita bwino powasamalira, monga nyali younikira m'malo a mdima, kufikira kukacha, nikauka nthanda pa mtima yanu; ndi kudziwa ichi poyamba, kuti palibe chinenero cha lembo chitanthauzidwa pa chokha, pakuti kale lonse chinenero sichinadza ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula. Koma padakhalanso pakati pa anthuwo aneneri onama, monganso padzakhala aphunzitsi onama pakati pa inu, amene adzalowa nayo m'tseri mipatuko yotayikitsa, nadzakana Ambuye amene adawagula, nadzadzitengera iwo okha chitayiko chakudza msanga. Ndipo ambiri adzatsata zonyansa zao; chifukwa cha iwo njira ya choonadi idzanenedwa zamwano. Ndipo m'chisiriro adzakuyesani malonda ndi mau onyenga; amene chiweruzo chao sichinachedwa ndi kale lomwe, ndipo chitayiko chao sichiodzera. Pakuti ngati Mulungu sanalekerera angelo adachimwawo, koma anawaponya kundende nawaika kumaenje a mdima, asungike akaweruzidwe; ndipo sanalekerera dziko lapansi lakale, koma anasunga Nowa mlaliki wa chilungamo, ndi anzake asanu ndi awiri, pakulitengera dziko la osapembedza chigumula; ndipo pakuisandutsa makala midzi ya Sodomu ndi Gomora anaitsutsa poigwetsa, ataiika chitsanzo cha kwa iwo akakhala osapembedza; ndipo anapulumutsa Loti wolungamayo, wolema mtima ndi mayendedwe onyansa a oipa aja (pakuti wolungamayo pokhala pakati pao. Ndi kuona ndi kumva zao, anadzizunzira moyo wake wolungama tsiku ndi tsiku ndi ntchito zao zosaweruzika). Ambuye adziwa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe; koma makamaka iwo akutsata za thupi, m'chilakolako cha zodetsa, napeputsa chilamuliro; osaopa kanthu, otsata chifuniro cha iwo eni, santhunthumira kuchitira mwano akulu aulemerero; popeza angelo, angakhale awaposa polimbitsa mphamvu, sawaneneza kwa Ambuye mlandu wakuchita mwano. Koma awo, ngati zamoyo zopanda nzeru, nyama zobadwa kuti zikodwe ndi kuonongedwa, akuchitira mwano pa zinthu osazidziwa, adzaonongeka m'kuononga kwao, ochitidwa zoipa kulipira kwa chosalungama; anthu akuyesera chowakondweretsa kudyerera usana; ndiwo mawanga ndi zilema, akudyerera m'madyerero achikondi ao, pamene akudya nanu; okhala nao maso odzala ndi chigololo, osakhoza kuleka uchimo, kunyengerera iwo a moyo wosakhazikika; okhala nao mtima wozolowera kusirira; ana a temberero; posiya njira yolunjika, anasokera, atatsata njira ya Balamu mwana wa Beori, amene anakonda mphotho ya chosalungama; koma anadzudzulidwa pa kulakwa kwake mwini; bulu wopanda mau, wolankhula ndi mau a munthu, analetsa kuyaluka kwa mneneriyo. Iwo ndiwo akasupe opanda madzi, nkhungu yokankhika ndi mkuntho; amene mdima wakuda bii uwasungikira. Pakuti polankhula mau otukumuka opanda pake, anyengerera pa zilakolako za thupi, ndi zonyansa, iwo amene adayamba kupulumukira a mayendedwe olakwawo; ndi kuwalonjezera iwo ufulu, pokhala iwo okha ali akapolo a chivundi; pakuti iye amene munthu agonjedwa naye, ameneyonso adzakhala kapolo wake. Pakuti ngati, adatha kuthawa zodetsa za dziko lapansi mwa chizindikiritso cha Ambuye ndi Mpulumutsi Yesu Khristu, akondwanso nazo, nagonjetsedwa, zotsiriza zao zidzaipa koposa zoyambazo. Pakuti pakadakhala bwino kwa iwo akadakhala osazindikira njira ya chilungamo, ndi poizindikira, kubwerera kutaya lamulo lopatulika lopatsidwa kwa iwo. Chidawayenera iwo cha nthanthi yoona, Galu wabwerera kumasanzi ake, ndi nkhumba idasambayi yabwerera kukunkhulira m'thope. Okondedwa, uyu ndiye kalata wachiwiri ndilembera kwa inu tsopano; mwa onse awiri nditsitsimutsa mtima wanu woona ndi kukukumbutsani; kuti mukumbukire mau onenedwa kale ndi aneneri oyera, ndi lamulo la Ambuye ndi Mpulumutsi, mwa atumwi anu; ndi kuyamba kuchizindikira ichi kuti masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni, ndi kunena, Lili kuti lonjezano la kudza kwake? Pakuti kuyambira kuja makolo adamwalira zonse zikhala monga chiyambire chilengedwe. Pakuti ichi aiwala dala, kuti miyamba inakhala kale lomwe, ndi dziko lidaungika ndi madzi ndi mwa madzi, pa mau a Mulungu; mwa izi dziko lapansi la masiku aja, pomizika ndi madzi, lidaonongeka; koma miyamba ndi dziko la masiku ano, ndi mau omwewo zaikika kumoto, zosungika kufikira tsiku la chiweruzo ndi chionongeko cha anthu osapembedza. Koma ichi chimodzi musaiwale, okondedwa inu, kuti tsiku limodzi likhala kwa Ambuye ngati zaka chikwi, ndi zaka chikwi ngati tsiku limodzi. Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena aonongeke, koma kuti onse afike kukulapa. Koma tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala; m'mene miyamba idzapita ndi chibumo chachikulu, ndi zam'mwamba zidzakanganuka ndi kutentha kwakukulu, ndipo dziko ndi ntchito zili momwemo zidzatenthedwa. Popeza izi zonse zidzakanganuka kotero, muyenera inu kukhala anthu otani nanga, m'mayendedwe opatulika ndi m'chipembedzo, akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Mulungu, m'menemo miyamba potentha moto idzakanganuka, ndi zam'mwamba zidzasungunuka ndi kutentha kwakukulu. Koma monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano m'menemo mukhalitsa chilungamo. Momwemo, okondedwa, popeza muyembekeza izi, chitani changu kuti mupezedwe ndi Iye mumtendere, opanda banga ndi opanda chilema. Ndipo yesani kulekerera kwa Ambuye wathu chipulumutso; monganso mbale wathu wokondedwa Paulo, monga mwa nzeru zopatsidwa kwa iye, anakulemberani; monganso m'akalata ake onse pokamba momwemo za izi; m'menemo muli zina zovuta kuzizindikira, zimene anthu osaphunzira ndi osakhazikika apotoza, monganso atero nao malembo ena, ndi kudziononga nao eni. Inu, tsono, okondedwa, pozizindikiratu izi, chenjerani, kuti potengedwa ndi kulakwa kwa iwo osaweruzika, mungagwe kusiya chikhazikiko chanu. Koma kulani m'chisomo ndi chizindikiritso cha Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu; kwa Iye kukhale ulemerero, tsopano ndi nthawi zonse. Amen. Chimene chinaliko kuyambira pachiyambi, chimene tidachimva, chimene tidachiona m'maso mwathu, chimene tidachipenyerera, ndipo manja athu adachigwira cha Mau a moyo, (ndipo moyowo unaonekera, ndipo tidaona, ndipo tichita umboni, ndipo tikulalikirani moyo wosathawo, umene unali kwa Atate, nuonekera kwa ife); chimene tidachiona, ndipo tidachimva, tikulalikirani inunso, kuti inunso mukayanjane pamodzi ndi ife; ndipo chiyanjano chathu chilinso ndi Atate, ndipo ndi Mwana wake Yesu Khristu; ndipo izi tilemba ife, kuti chimwemwe chathu chikwaniridwe. Ndipo uwu ndi uthenga tidaumva kwa Iye, ndipo tiulalikira kwa inu, kuti Mulungu ndiye kuunika, ndipo mwa Iye monse mulibe mdima. Tikati kuti tiyanjana ndi Iye, ndipo tiyenda mumdima, tinama, ndipo sitichita choonadi; koma ngati tiyenda m'kuunika, monga Iye ali m'kuunika, tiyanjana wina ndi mnzake, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse. Tikati kuti tilibe uchimo, tidzinyenga tokha, ndipo mwa ife mulibe choonadi. Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chilichonse. Tikanena kuti sitidachimwa, timuyesa Iye wonama, ndipo mau ake sakhala mwa ife. Tiana tanga, izi ndikulemberani, kuti musachimwe. Ndipo akachimwa wina, Nkhoswe tili naye kwa Atate, ndiye Yesu Khristu wolungama; ndipo Iye ndiye chiombolo cha machimo athu; koma wosati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi. Ndipo umo tizindikira kuti tamzindikira Iye, ngati tisunga malamulo ake. Iye wakunena kuti, Ndimdziwa Iye, koma wosasunga malamulo ake, ali wabodza, ndipo mwa iye mulibe choonadi; koma iye amene akasunga mau ake, mwa iyeyu zedi chikondi cha Mulungu chathedwa. M'menemo tizindikira kuti tili mwa Iye; iye wakunena kuti akhala mwa Iye, ayeneranso mwini wake kuyenda monga anayenda Iyeyo. Okondedwa, sindikulemberani lamulo latsopano, komatu lamulo lakale limene munali nalo kuyambira pa chiyambi; lamulo lakalelo ndilo mau amene mudawamva. Ndikulemberaninso lamulo latsopano, ndicho chimene chili choona mwa Iye ndi mwa inu; kuti mdima ulinkupita, ndi kuunika koona kwayamba kuwala. Iye amene anena kuti ali m'kuunika, namuda mbale wake, ali mumdima kufikira tsopano lino. Iye amene akonda mbale wake akhala m'kuunika, ndipo mwa iye mulibe chokhumudwitsa. Koma iye wakumuda mbale wake ali mumdima, nayenda mumdima, ndipo sadziwa kumene amukako, pakuti mdima wamdetsa maso ake. Ndikulemberani, tiana, popeza machimo adakhululukidwa kwa inu mwa dzina lake. Ndikulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndikulemberani, anyamata, popeza mwamlaka woipayo. Ndakulemberani, ana, popeza mwazindikira Atate. Ndakulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndakulemberani, anyamata, popeza muli amphamvu, ndi mau a Mulungu akhala mwa inu, ndipo mwamlaka woipayo. Musakonde dziko lapansi, kapena za m'dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichili mwa iye. Pakuti chilichonse cha m'dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma kudziko lapansi. Ndipo dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala kunthawi yonse. Ana inu, ndi nthawi yotsiriza iyi; ndipo monga mudamva kuti wokana Khristu akudza, ngakhale tsopano alipo okana Khristu ambiri; mwa ichi tizindikira kuti ndi nthawi yotsirizira iyi. Anatuluka mwa ife, komatu sanali a ife; pakuti akadakhala a ife akadakhalabe ndi ife, koma kudatero kuti aonekere kuti sali onse a ife. Ndipo inu muli nako kudzoza kochokera kwa Woyerayo, ndipo mudziwa zonse. Sindinakulemberani chifukwa simudziwa choonadi, koma chifukwa muchidziwa, ndi chifukwa kulibe bodza lochokera kwa choonadi. Wabodza ndani, koma iye wokanayo kuti Yesu siali Khristu? Iye ndiye wokana Khristu, amene akana Atate ndi Mwana. Yense wakukana Mwana, alibe Atate; wovomereza Mwana ali ndi Atatenso. Koma inu, chimene munachimva kuyambira pachiyambi chikhale mwa inu. Ngati chikhala mwa inu chimene mudachimva kuyambira pachiyambi, inunso mudzakhalabe mwa Mwana, ndi mwa Atate. Ndipo ili ndi lonjezano Iye anatilonjezera ife, ndiwo moyo wosatha. Izi ndakulemberani za iwo akusokeretsa inu. Ndipo inu, kudzoza kumene munalandira kuchokera kwa Iye, kukhala mwa inu, ndipo simusowa kuti wina akuphunzitseni; koma monga kudzoza kwake kukuphunzitsani za zinthu zonse, ndipo kuli koona, sikuli bodza ai, ndipo monga kudaphunzitsa inu, mukhale mwa Iye. Ndipo tsopano, tiana, khalani mwa Iye; kuti akaonekere Iye tikakhale nako kulimbika mtima, osachita manyazi kwa Iye pa kudza kwake. Ngati mudziwa kuti ali wolungama, muzindikira kuti aliyensenso wakuchita chilungamo abadwa kuchokera mwa Iye. Taonani, chikondicho Atate watipatsa, kuti titchedwe ana a Mulungu; ndipo tili ife otere. Mwa ichi dziko lapansi silizindikira ife, popeza silimzindikira Iye. Okondedwa, tsopano tili ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Tidziwa kuti, pa kuoneka Iye, tidzakhala ofanana ndi Iye, Pakuti tidzamuona Iye monga ali. Ndipo yense wakukhala nacho chiyembekezo ichi pa Iye, adziyeretsa yekha, monga Iyeyu ali Woyera. Yense wakuchita tchimo achitanso kusaweruzika; ndipo tchimo ndilo kusaweruzika. Ndipo mudziwa kuti Iyeyu anaonekera kudzachotsa machimo; ndipo mwa Iye mulibe tchimo. Yense wakukhala mwa Iye sachimwa; yense wakuchimwa sanamuona Iye, ndipo sanamdziwa Iye. Tiana, munthu asasokeretse inu; iye wakuchita cholungama ali wolungama, monga Iyeyu ali wolungama: iye wochita tchimo ali wochokera mwa mdierekezi, chifukwa mdierekezi amachimwa kuyambira pachiyambi. Kukachita ichi Mwana wa Mulungu adaonekera, ndiko kuti akaononge ntchito za mdierekezi. Yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachita tchimo, chifukwa mbeu yake ikhala mwa iye; ndipo sakhoza kuchimwa, popeza wabadwa kuchokera mwa Mulungu. M'menemo aoneka ana a Mulungu, ndi ana a mdierekezi: yense wosachita chilungamo siali wochokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wake. Pakuti uwu ndi uthenga mudaumva kuyambira pachiyambi, kuti tikondane wina ndi mnzake: osati monga Kaini anali wochokera mwa woipayo, namupha mbale wake. Ndipo anamupha Iye chifukwa ninji? Popeza ntchito zake zinali zoipa, ndi za mbale wake zolungama. Musazizwe, abale, likadana nanu dziko lapansi. Ife tidziwa kuti tachokera kutuluka muimfa kulowa m'moyo, chifukwa tikondana ndi abale. Iye amene sakonda akhala muimfa. Yense wakudana ndi mbale wake ali wakupha munthu; ndipo mudziwa kuti wakupha munthu aliyense alibe moyo wosatha wakukhala mwa iye. Umo tizindikira chikondi, popeza Iyeyu anapereka moyo wake chifukwa cha ife; ndipo ife tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale. Koma iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, naona mbale wake ali wosowa ndi kutsekereza chifundo chake pommana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji? Tiana, tisakonde ndi mau, kapena ndi lilime, komatu ndi kuchita ndi m'choonadi. Umo tidzazindikira kuti tili ochokera m'choonadi, ndipo tidzakhazikitsa mtima wathu pamaso pake, m'mene monse mtima wathu utitsutsa; chifukwa Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu, nazindikira zonse. Okondedwa, mtima wathu ukapanda kutitsutsa, tili nako kulimbika mtima mwa Mulungu; ndipo chimene chilichonse tipempha, tilandira kwa Iye, chifukwa tisunga malamulo ake, ndipo tichita zomkondweretsa pamaso pake. Ndipo lamulo lake ndi ili, kuti tikhulupirire dzina la Mwana wake Yesu Khristu, ndi kukondana wina ndi mnzake monga anatilamulira. Ndipo munthu amene asunga malamulo ake akhala mwa Iye, ndi Iye mwa munthuyo. Ndipo m'menemo tizindikira kuti akhala mwa ife, kuchokera mwa Mzimu amene anatipatsa ife. Okondedwa, musamakhulupirira mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ichokera mwa Mulungu: popeza aneneri onyenga ambiri anatuluka kulowa m'dziko lapansi. M'menemo muzindikira Mzimu wa Mulungu: mzimu uliwonse umene uvomereza kuti Yesu Khristu anadza m'thupi, uchokera mwa Mulungu; ndipo mzimu uliwonse umene suvomereza Yesu suchokera kwa Mulungu; ndipo uwu ndiwo mzimu wa wokana Khristu umene mudamva kuti ukudza; ndipo ulimo m'dziko lapansi tsopano lomwe, Inu ndinu ochokera mwa Mulungu, tiana, ndipo munailaka; pakuti Iye wakukhala mwa inu aposa iye wakukhala m'dziko lapansi. Iwo ndiwo ochokera m'dziko lapansi; mwa ichi alankhula monga ochokera m'dziko lapansi, ndipo dziko lapansi liwamvera. Ife ndife ochokera mwa Mulungu; iye amene azindikira Mulungu atimvera; iye wosachokera mwa Mulungu satimvera ife. Momwemo tizindikira mzimu wa choonadi, ndi mzimu wa chisokeretso. Okondedwa, tikondane wina ndi mnzake: chifukwa kuti chikondi chichokera kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kuchokera kwa Mulungu, namzindikira Mulungu. Iye wosakonda sazindikira Mulungu; chifukwa Mulungu ndiye chikondi. Umo chidaoneka chikondi cha Mulungu mwa ife, kuti Mulungu anamtuma Mwana wake wobadwa yekha, alowe m'dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa Iye. Umo muli chikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti Iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wake akhale chiombolo chifukwa cha machimo athu. Okondedwa, ngati Mulungu anatikonda ife kotero, ifenso tiyenera kukondana wina ndi mnzake. Palibe munthu adamuona Mulungu nthawi iliyonse; tikakondana wina ndi mnzake, Mulungu akhala mwa ife, ndi chikondi chake chikhala changwiro mwa ife; m'menemo tizindikira kuti tikhala mwa Iye, ndi Iye mwa ife, chifukwa anatipatsako Mzimu wake. Ndipo ife tapenyera, ndipo tichita umboni kuti Atate anatuma Mwana akhale Mpulumutsi wa dziko lapansi. Iye amene adzavomereza kuti Yesu ali Mwana wa Mulungu, Mulungu akhala mwa iye, ndi iye mwa Mulungu. Ndipo ife tazindikira, ndipo takhulupirira chikondicho Mulungu ali nacho pa ife. Mulungu ndiye chikondi, ndipo iye amene akhala m'chikondi akhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu akhala mwa iye. M'menemo chikondi chathu chikhala changwiro kuti tikhale nako kulimbika mtima m'tsiku la mlandu; chifukwa monga Iyeyu ali, momwemo tili ife m'dziko lino lapansi. Mulibe mantha m'chikondi; koma chikondi changwiro chitaya kunja mantha, popeza mantha ali nacho chilango, ndipo wamanthayo sakhala wangwiro m'chikondi. Tikonda ife, chifukwa anayamba Iye kutikonda. Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wake, ali wabodza: pakuti iye wosakonda mbale wake amene wamuona, sakhoza kukonda Mulungu amene sanamuona. Ndipo lamulo ili tili nalo lochokera kwa Iye, kuti iye amene akonda Mulungu akondenso mbale wake. Yense wokhulupirira kuti Yesu ndiye Khristu wabadwa kuchokera kwa Mulungu; ndipo yense wakukonda Iye amene anabala akondanso iye amene anabadwa wochokera mwa Iye. Umo tizindikira kuti tikonda ana a Mulungu, pamene tikonda Mulungu, ndi kuchita malamulo ake. Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa. Pakuti chilichonse chabadwa mwa Mulungu chiligonjetsa dziko lapansi; ndipo ichi ndi chigonjetso tichigonjetsa nacho dziko lapansi, ndicho chikhulupiriro chathu. Koma ndani iye wogonjetsa dziko lapansi, koma iye amene akhulupirira kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu? Iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi, ndiye Yesu Khristu; wosati ndi madzi okha, koma ndi madzi ndi mwazi. Ndipo Mzimu ndiye wakuchita umboni, chifukwa Mzimu ndiye choonadi. Pakuti pali atatu akuchita umboni, Mzimu, ndi madzi, ndi mwazi; ndipo iwo atatu ali mmodzi. Ngati tilandira umboni wa anthu, umboni wa Mulungu uposa; chifukwa umboni wa Mulungu ndi uwu, kuti anachita umboni za Mwana wake. Iye amene amkhulupirira Mwana wa Mulungu ali nao umboni mwa iye; iye wosakhulupirira Mulungu anamuyesa Iye wonama; chifukwa sanakhulupirira umboni wa Mulungu anauchita wa Mwana wake. Ndipo uwu ndi umboniwo, kuti Mulungu anatipatsa ife moyo wosatha, ndipo moyo umene uli mwa Mwana wake. Iye wakukhala ndi Mwana ali nao moyo; wosakhala ndi Mwana wa Mulungu alibe moyo. Izi ndakulemberani, kuti mudziwe kuti muli ndi moyo wosatha, inu amene mukhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu. Ndipo uku ndi kulimbika mtima kumene tili nako kwa Iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera; ndipo ngati tidziwa kuti atimvera chilichonse tichipempha, tidziwa kuti tili nazo izi tazipempha kwa Iye. Wina akaona mbale wake alikuchimwa tchimo losati la kuimfa, apemphere Mulungu, ndipo Iye adzampatsira moyo wa iwo akuchita machimo osati a kuimfa. Pali tchimo la kuimfa: za ililo sindinena kuti mupemphere. Chosalungama chilichonse chili uchimo; ndipo pali tchimo losati la kuimfa. Tidziwa kuti yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachimwa, koma iye wobadwa kuchokera mwa Mulungu adzisunga yekha, ndipo woipayo samkhudza. Tidziwa kuti tili ife ochokera mwa Mulungu, ndipo dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo. Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife chidziwitso, kuti tizindikire Woonayo, ndipo tili mwa Woonayo, mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iye ndiye Mulungu woona ndi moyo wosatha. Tiana, dzisungireni nokha kupewa mafano. Mkuluyo kwa mkazi womveka wosankhika, ndi ana ake, amene ine ndikondana nao m'choonadi; ndipo si ine ndekha, komanso onse akuzindikira choonadi; chifukwa cha choonadi chimene chikhala mwa ife, ndipo chidzakhala ndi ife ku nthawi yosatha: Chisomo, chifundo, mtendere zikhale ndi ife zochokera kwa Mulungu Atate, ndi kwa Yesu Khristu Mwana wa Atate, m'choonadi ndi m'chikondi. Ndakondwera kwakukulu kuti ndapeza ena a ana anu alikuyenda m'choonadi, monga tinalandira lamulo lochokera kwa Atate. Ndipo tsopano ndikupemphani, mkazi womveka inu, wosati monga kukulemberani lamulo latsopano, koma lomwelo tinali nalo kuyambira pachiyambi, kuti tikondane wina ndi mnzake. Ndipo chikondi ndi ichi, kuti tiyende monga mwa malamulo ake. Ili ndi lamulolo, monga mudalimva kuyambira pachiyambi, kuti mukayende momwemo. Pakuti onyenga ambiri adatuluka kulowa m'dziko lapansi, ndiwo amene savomereza kuti Yesu Khristu anadza m'thupi. Ameneyo ndiye wonyenga ndi wokana Khristu. Mudzipenyerere nokha, kuti mungataye zimene tazichita, koma kuti mulandire mphotho yokwanira. Yense wakupitirira, wosakhala m'chiphunzitso cha Khristu, alibe Mulungu; iye wakukhala m'chiphunzitso, iyeyo ali nao Atate ndi Mwana. Munthu akadza kwa inu, wosatenga chiphunzitso ichi, musamlandire iye kunyumba, ndipo musampatse moni. Pakuti iye wakumpatsa moni ayanjana nazo ntchito zake zoipa. Pokhala ndili nazo zambiri zakukulemberani, sindifuna kuchita ndi kalata ndi kapezi; koma ndiyembekeza kudza kwa inu, ndi kulankhula popenyana, kuti chimwemwe chanu chikwanire. Akupereka moni ana a mbale wanu wosankhika. Mkuluyo kwa Gayo wokondedwayo, amene ndikondana naye m'choonadi. Wokondedwa, ndipemphera kuti pa zonse ulemere, nukhale bwino, monga mzimu wako ulemera. Pakuti ndinakondwera kwakukulu, pofika abale ndi kuchita umboni za choonadi chako, monga umayenda m'choonadi. Ndilibe chimwemwe choposa ichi, chakuti ndimva za ana anga kuti alikuyenda m'choonadi. Wokondedwa, uchita chokhulupirika nacho chilichonse, uwachitira abale ndi alendo omwe; amene anachita umboni za chikondi chako pamaso pa Mpingo; ngati uwaperekeza amenewo pa ulendo wao koyenera Mulungu, udzachita bwino: pakuti chifukwa cha dzinali anatuluka, osalandira kanthu kwa amitundu. Chifukwa chake ife tiyenera kulandira otere, kuti tikakhale othandizana nacho choonadi. Ndalemba kanthu kwa Mpingo; komatu Diotrefe uja, wofuna kukhala wamkulu wa iwo, satilandira ife. Momwemo, ndikadza ine, ndidzakumbutsa ntchito zake zimene achitazi, zakunena zopanda pake pa ife ndi mau oipa; ndipo popeza izi sizimkwanira, salandira abale iye yekha, ndipo ofuna kuwalandira awaletsa, nawataya kunja powatulutsa mu Mpingo. Wokondedwa, usatsanza chili choipa komatu chimene chili chokoma. Iye wakuchita chokoma achokera kwa Mulungu; iye wakuchita choipa sanamuona Mulungu. Demetrio, adamchitira umboni anthu onse, ndi choonadi chomwe; ndipo ifenso tichita umboni; ndipo udziwa kuti umboni wathu uli woona. Ndinali nazo zambiri za kukulembera, komatu sindifuna kukulembera ndi kapezi ndi peni; koma ndiyembekeza kukuona iwe msanga, ndipo tidzalankhula popenyana. Mtendere ukhale nawe. Akupereka moni abwenzi. Upereke moni kwa abwenzi ndi kutchula maina ao. Yuda, kapolo wa Yesu Khristu, ndi mbale wa Yakobo, kwa iwo oitanidwa, okondedwa mwa Mulungu Atate, ndi osungidwa ndi Yesu Khristu: Chifundo ndi mtendere ndi chikondi zikuchulukireni. Okondedwa, pakuchita changu chonse chakukulemberani za chipulumutso cha ife tonse, ndafulumidwa mtima ine kukulemberani ndi kudandaulira kuti mulimbanetu chifukwa cha chikhulupiriro chapatsidwa kamodzi kwa oyera mtima. Pakuti pali anthu ena anakwawira m'tseri, ndiwo amene aja adalembedwa maina ao kale, kukalandira chitsutso ichi, anthu osapembedza, akusandutsa chisomo cha Mulungu wathu chikhale chilakolako chonyansa, nakaniza Mfumu wayekha, ndi Ambuye wathu, Yesu Khristu. Koma ndifuna kukukumbutsani mungakhale munadziwa zonse kale, kuti Ambuye, atapulumutsa mtundu wa anthu ndi kuwatulutsa m'dziko la Ejipito, anaononganso iwo osakhulupirira. Angelonso amene sanasunga chikhalidwe chao choyamba, komatu anasiya pokhala paopao, adawasunga m'ndende zosatha pansi pa mdima, kufikira chiweruziro cha tsiku lalikulu. Monga Sodomu ndi Gomora, ndi midzi yakuizungulira, potsatana nayoyo, idadzipereka kudama, ndi kutsata zilakolako zachilendo, iikidwa chitsanzo, pakuchitidwa chilango cha moto wosatha. Momwemonso iwo m'kulota kwao adetsa matupi ao, napeputsa ufumu, nachitira mwano maulemerero. Koma Mikaele mkulu wa angelo, pakuchita makani ndi mdierekezi anatsutsana za thupi la Mose, sanalimbika mtima kumtchulira chifukwa chomchitira mwano, koma anati, Ambuye akudzudzule. Koma iwowa zimene sazidziwa azichitira mwano; ndipo zimene azizindikira chibadwire, monga zamoyo zopanda nzeru, mu izi atayika. Tsoka kwa iwo! Pakuti anayenda m'njira ya Kaini, ndipo anadziononga m'chisokero cha Balamu chifukwa cha kulipira, natayika m'chitsutsano cha Kora. Iwo ndiwo okhala mawanga pa maphwando anu a chikondano, pakudya nanu pamodzi, akudziweta okha opanda mantha; mitambo yopanda madzi, yotengekatengeka ndi mphepo; mitengo ya masika yopanda zipatso, yofafa kawiri, yozuka mizu; mafunde oopsa a nyanja, akuwinduka thovu la manyazi a iwo okha; nyenyezi zosokera, zimene mdima wakuda bii udazisungikira kosatha. Ndipo kwa iwo, Enoki, wachisanu ndi chiwiri kuyambira kwa Adamu, ananenera kuti, Taona, wadza Ambuye ndi oyera ake zikwi makumi, kudzachitira onse chiweruziro, ndi kutsutsa osapembedza onse, pa ntchito zao zonse zosapembedza, ndi pa zolimba zimene ochimwa osapembedza adalankhula pa Iye. Amenewo ndiwo odandaula, oderera, akuyenda monga mwa zilakolako zao (ndipo pakamwa pao alankhula zazikuluzikulu), akutama anthu chifukwa cha kupindula nako. Koma inu, abale, mukumbukire mau onenedwa kale ndi atumwi a Ambuye wathu Yesu Khristu; kuti ananena nanu, Pa nthawi yotsiriza padzakhala otonza, akuyenda monga mwa zilakolako zosapembedza za iwo okha. Iwo ndiwo opatukitsa, anthu a makhalidwe achibadwidwe, osakhala naye Mzimu. Koma inu, okondedwa, podzimangirira nokha pa chikhulupiriro chanu choyeretsetsa, ndi kupemphera mu Mzimu Woyera, mudzisunge nokha m'chikondi cha Mulungu, ndi kulindira chifundo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, kufikira moyo wosatha. Ndipo ena osinkhasinkha muwachitire chifundo, koma ena muwapulumutse ndi kuwakwatula kumoto; koma ena muwachitire chifundo ndi mantha, nimudane naonso malaya ochitidwa mawanga ndi thupi. Ndipo kwa Iye amene akhoza kukudikirani mungakhumudwe, ndi kukuimikani pamaso pa ulemerero wake opanda chilema m'kukondwera, kwa Mulungu wayekha, Mpulumutsi wathu, mwa Yesu Khristu Ambuye wathu, zikhale ulemerero, ukulu, mphamvu, ndi ulamuliro zisanayambe nthawi, ndi tsopano, ndi kufikira nthawi zonse. Amen. Chivumbulutso cha Yesu Khristu, chimene Mulungu anamvumbulutsira achionetsera akapolo ake, ndicho cha izi ziyenera kuchitika posachedwa: ndipo potuma mwa mngelo wake anazindikiritsa izi kwa kapolo wake Yohane; amene anachita umboni za mau a Mulungu, ndi za umboni wa Yesu Khristu, zonse zimene adaziona. Wodala iye amene awerenga, ndi iwo amene akumva mau a chinenerocho, nasunga zolembedwa momwemo; pakuti nthawi yayandikira. Yohane kwa Mipingo isanu ndi iwiri m'Asiya: Chisomo kwa inu ndi mtendere, zochokera kwa Iye amene ali, ndi amene adali, ndi amene alinkudza; ndi kwa mizimu isanu ndi iwiri yokhala kumpando wachifumu wake; ndi kwa Yesu Khristu, mboni yokhulupirikayo, wobadwa woyamba wa akufa, ndi mkulu wa mafumu a dziko lapansi. Kwa Iye amene atikonda ife, natimasula kumachimo athu ndi mwazi wake; natiyesa ife ufumu tikhale ansembe a Mulungu ndiye Atate wake; kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu kufikira nthawi za nthawi. Amen. Taonani, adza ndi mitambo; ndipo diso lililonse lidzampenya Iye, iwonso amene anampyoza; ndipo mafuko onse a pa dziko adzamlira Iye. Terotu. Amen. Ine ndine Alefa ndi Omega, ati Ambuye Mulungu, amene ali, amene adali, ndi amene alinkudza, Wamphamvuyonse. Ine Yohane, mbale wanu ndi woyanjana nanu m'chisautso ndi ufumu ndi chipiriro zokhala mwa Yesu, ndinakhala pa chisumbu chotchedwa Patimosi, chifukwa cha mau a Mulungu ndi umboni wa Yesu. Ndinagwidwa ndi Mzimu tsiku la Ambuye, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau akulu, ngati a lipenga, ndi kuti, Chimene upenya, lemba m'buku, nulitumize kwa Mipingo isanu ndi iwiri, ku Efeso, ndi ku Smirina, ndi ku Pergamo, ndi ku Tiatira, ndi ku Sardi, ndi ku Filadelfiya, ndi ku Laodikea. Ndipo ndinacheuka kuona wonena mau amene adalankhula ndi ine. Ndipo nditacheuka ndinaona zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri zagolide; ndipo pakati pa zoikapo nyalizo wina wonga Mwana wa Munthu atavala chofikira kumapazi ake, atamangira lamba lagolide pachifuwa. Ndipo tsitsi la pamutu pake linali loyera ngati ubweya woyera, ngati chipale chofewa; ndi maso ake ngati lawi la moto; ndi mapazi ake ngati mkuwa wonyezimira, ngati woyengeka m'ng'anjo; ndi mau ake ngati mkokomo wa madzi ambiri. Ndipo m'dzanja lake lamanja munali nyenyezi zisanu ndi ziwiri; ndi m'kamwa mwake mudatuluka lupanga lakuthwa konsekonse; ndipo nkhope yake ngati dzuwa lowala mu mphamvu yake. Ndipo pamene ndinamuona Iye, ndinagwa pa mapazi ake ngati wakufa; ndipo anaika dzanja lake lamanja pa ine, nati, Usaope, Ine ndine Woyamba ndi Wotsiriza, ndi Wamoyoyo; ndipo ndinali wakufa, ndipo taona, ndili wamoyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo ndili nazo zofungulira za imfa ndi dziko la akufa. Chifukwa chake lemba zimene unaziona, ndi zimene zilipo, ndi zimene zidzaoneka m'tsogolomo; chinsinsi cha nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene unaziona pa dzanja langa lamanja, ndi zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri zagolide: nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndizo angelo a Mipingo isanu ndi iwiri; ndipo zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri ndizo Mipingo isanu ndi iwiri. Kwa mngelo wa Mpingo wa ku Efeso lemba: Izi azinena Iye amene agwira nyenyezi zisanu ndi ziwiri m'dzanja lake lamanja, Iye amene ayenda pakati pa zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri zagolide: Ndidziwa ntchito zako, ndi chilemetso chako ndi chipiriro chako ndi kuti sukhoza kulola oipa, ndipo unayesa iwo amene adzitcha okha atumwi, osakhala atumwi, nuwapeza onama; ndipo uli nacho chipiriro, ndipo walola chifukwa cha dzina langa, wosalema. Koma ndili nako kanthu kotsutsana ndi iwe, kuti unataya chikondi chako choyamba. Potero kumbukira kumene wagwerako, nulape, nuchite ntchito zoyamba; koma ngati sutero, ndidzadza kwa iwe, ndipo ndidzatunsa choikapo nyali chako, kuchichotsa pamalo pake, ngati sulapa. Koma ichi uli nacho, kuti udana nazo ntchito za Anikolai, zimene Inenso ndidana nazo. Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye amene alakika ndidzampatsa kudya za ku mtengo wa moyo umene uli m'Paradaiso wa Mulungu. Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Smirina lemba: Izi anena woyamba ndi wotsiriza, amene anakhala wakufa, nakhalanso ndi moyo: Ndidziwa chisautso chako, ndi umphawi wako (komatu uli wachuma), ndi mwano wa iwo akunena za iwo okha kuti ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu sunagoge wa Satana. Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, mdierekezi adzaponya ena a inu m'nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi. Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo. Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Iye amene alakika sadzachitidwa choipa ndi imfa yachiwiri. Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Pergamo lemba: Izi anena Iye wokhala nalo lupanga lakuthwa konsekonse: Ndidziwa kumene ukhalako kuja kuli mpando wachifumu wa Satana; ndipo ugwira dzina langa, osakaniza chikhulupiriro changa, angakhale m'masiku a Antipa, mboni yanga, wokhulupirika wanga, amene anaphedwa pali inu, kuja akhalako Satana. Komatu ndili nazo zinthu pang'ono zotsutsana ndi iwe, popeza uli nao komweko akugwira chiphunzitso cha Balamu, amene anaphunzitsa Balaki aponye chokhumudwitsa pamaso pa ana a Israele, kuti adye zoperekedwa nsembe kwa mafano, nachite chigololo. Kotero uli nao akugwira chiphunzitso cha Anikolai momwemonso. Chifukwa chake lapa; ukapanda kutero ndidza kwa iwe posachedwa, ndipo ndidzachita nao nkhondo ndi lupanga la m'kamwa mwanga. Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye wolakika, ndidzampatsa mana obisika, ndipo ndidzampatsa mwala woyera, ndi pa mwalawo dzina latsopano lolembedwapo, wosalidziwa munthu aliyense koma iye wakuulandira. Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Tiatira lemba: Izi azinena Mwana wa Mulungu, wakukhala nao maso ake ngati lawi la moto, ndi mapazi ake ngati mkuwa wonyezimira: Ndidziwa ntchito zako, ndi chikondi, ndi chikhulupiriro, ndi utumiki, ndi chipiriro chako, ndi kuti ntchito zako zotsiriza zichuluka koposa zoyambazo. Komatu ndili nako kotsutsana ndi iwe, kuti ulola mkazi Yezebele, wodzitcha yekha mneneri; ndipo aphunzitsa, nasocheretsa akapolo anga, kuti achite chigololo ndi kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano. Ndipo ndampatsa iye nthawi kuti alape; koma safuna kulapa kusiyana nacho chigololo chake. Taona, ndimponya iye pakama, ndi iwo akuchita chigololo naye kuwalonga m'chisautso chachikulu, ngati salapa iwo ndi kuleka ntchito zake. Ndipo ndidzaononga ana ake ndi imfa; ndipo idzazindikira Mipingo yonse kuti Ine ndine Iye amene ayesa impso ndi mitima; ndipo ndidzaninkha kwa yense wa inu monga mwa ntchito zanu. Koma ndinena kwa inu, kwa otsala a ku Tiatira, onse amene alibe chiphunzitso ichi, amene sanazindikira zakuya za Satana, monga anena, Sindikusanjikizani katundu wina. Koma chimene muli nacho, gwirani kufikira ndikadza. Ndipo iye amene alakika, ndi iye amene asunga ntchito zanga kufikira chitsiriziro, kwa iye ndidzapatsa ulamuliro wa pa amitundu; ndipo adzawalamulira ndi ndodo yachitsulo, monga zotengera za woumba mbiya ziphwanyika mapale; monga Inenso ndalandira kwa Atate wanga; ndipo ndidzampatsa iye nthanda. Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Sardi lemba: Izi anena Iye wakukhala nayo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri: Ndidziwa ntchito zako, kuti uli nalo dzina lakuti uli ndi moyo, ndipo uli wakufa. Khala wodikira, ndipo limbitsa zotsalira zimene zinafuna kufa; pakuti sindinapeza ntchito zako zakufikira pamaso pa Mulungu wanga. Chifukwa chake kumbukira umo unalandira nunamvamo; nusunge nulape. Ukapanda kudikira tsono, ndidzafika ngati mbala, ndipo sudzazindikira nthawi yake ndidzadza pa iwe. Komatu uli nao maina owerengeka m'Sardi, amene sanadetsa zovala zao; ndipo adzayenda ndi Ine m'zoyera; chifukwa ali oyenera. Iye amene alakika adzamveka motero zovala zoyera; ndipo sindidzafafaniza ndithu dzina lake m'buku la moyo, ndipo ndidzamvomereza dzina lake pamaso pa Atate wanga, ndi pamaso pa angelo ake. Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Filadelfiya lemba: Izi anena Iye amene ali Woyera, Iye amene ali Woona, Iye wakukhala nacho chifungulo cha Davide, Iye wotsegula, ndipo palibe wina atseka; Iye wotseka, ndipo palibe wina atsegula: Ndidziwa ntchito zako (taona, ndapatsa pamaso pako khomo lotseguka limene munthu sakhoza kutsekapo), kuti uli nayo mphamvu pang'ono, ndipo unasunga mau anga, osakana dzina langa. Taona, ndikupatsa ena otuluka m'sunagoge wa Satana akudzinenera okha ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu anama; taona, ndidzawadzetsa alambire pa mapazi ako, nazindikire kuti Ine ndakukonda. Popeza unasunga mau a chipiriro changa, Inenso ndidzakusunga kukulanditsa mu nthawi ya kuyesedwa, ikudza pa dziko lonse lapansi, kudzayesa iwo akukhala padziko. Ndidza msanga; gwira chimene uli nacho, kuti wina angalande korona wako. Iye wakupambana, ndidzamyesa iye mzati wa m'Kachisi wa Mulungu wanga, ndipo kutuluka sadzatulukamonso; ndipo ndidzalemba pa iye dzina la Mulungu wanga, ndi dzina la mzinda wa Mulungu wanga, la Yerusalemu watsopano, wotsika m'Mwamba, kuchokera kwa Mulungu wanga; ndi dzina langa latsopano. Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Laodikea lemba: Izi anena Ameni'yo, mboni yokhulupirika ndi yoona, woyamba wa chilengo cha Mulungu: Ndidziwa ntchito zako, kuti suli wozizira kapena wotentha: mwenzi utakhala wozizira kapena wotentha. Kotero, popeza uli wofunda, wosati wotentha kapena wozizira, ndidzakulavula m'kamwa mwanga. Chifukwa unena kuti ine ndine wolemera, ndipo chuma ndili nacho, osasowa kanthu; ndipo sudziwa kuti ndiwe watsoka, ndi wochititsa chifundo, ndi wosauka, ndi wakhungu, ndi wausiwa; ndikulangiza ugule kwa Ine golide woyengeka m'moto, kuti ukakhale wachuma, ndi zovala zoyera, kuti ukadziveke, ndi kuti manyazi a usiwa wako asaoneke; ndi mankhwala opaka m'maso mwako, kuti ukaone. Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero chita changu, nutembenuke mtima. Taona, ndaima pakhomo, ndigogoda; wina akamva mau anga nakatsegula pakhomo, ndidzalowa kwa iye, ndipo ndidzadya naye, ndi iye ndi Ine. Iye wakupambana, ndidzampatsa akhale pansi ndi Ine pa mpando wachifumu wanga, monga Inenso ndinalakika, ndipo ndinakhala pansi ndi Atate wanga pa mpando wachifumu wake. Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Zitatha izi ndinapenya, ndipo taonani, khomo lotseguka m'Mwamba, ndipo mau oyamba ndinawamva, ngati lipenga lakulankhula ndi ine, anati, Kwera kuno, ndipo ndidzakuonetsa zimene ziyenera kuchitika m'tsogolomo. Pomwepo ndinakhala mwa Mzimu; ndipo, taonani padaikika mpando wachifumu m'Mwamba ndi pa mpandowo padakhala wina; ndipo maonekedwe a Iye wokhalapo anafanana ndi mwala wa jaspi, ndi sardiyo; ndipo panali utawaleza wozinga mpando wachifumu, maonekedwe ake ngati smaragido. Ndipo pozinga mpando wachifumu mipando yachifumu makumi awiri mphambu inai, ndipo pa mipandoyo padakhala akulu makumi awiri mphambu anai, atavala zovala zoyera, ndi pamitu pao akorona agolide. Ndipo mu mpando wachifumu mudatuluka mphezi ndi mau ndi mabingu. Ndipo panali nyali zisanu ndi ziwiri za moto zoyaka kumpando wachifumu, ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu; ndipo kumpandowo, ngati nyanja yagalasi yonga krustalo; ndipo pakati pa mpandowo, ndi pozinga mpandowo, zamoyo zinai zodzala ndi maso kutsogolo ndi kumbuyo. Ndipo chamoyo choyamba chinafanana nao mkango, ndi chamoyo chachiwiri chinafanana ndi mwanawang'ombe, ndi chamoyo chachitatu chinali nayo nkhope yake ngati ya munthu, ndi chamoyo chachinai chidafanana ndi chiombankhanga chakuuluka. Ndipo zamoyozo zinai, chonse pa chokha chinali nao mapiko asanu ndi limodzi; ndipo zinadzala ndi maso pozinga ponse ndi m'katimo; ndipo sizipumula usana ndi usiku, ndi kunena, Woyera, woyera, woyera, Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, amene anali, amene ali, ndi amene alinkudza. Ndipo pamene zamoyozo zipereka ulemerero ndi ulemu ndi uyamiko kwa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, kwa Iye wakukhala ndi moyo kufikira nthawi za nthawi, akulu makumi awiri mphambu anai amagwa pansi pamaso pa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, namlambira Iye amene akhala ndi moyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo aponya pansi akorona ao kumpando wachifumu, ndi kunena, Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa. Ndipo ndinaona m'dzanja lamanja la Iye wakukhala pa mpando wachifumu buku lolembedwa m'kati ndi kunja kwake, losindikizika ndi zizindikiro zisanu ndi ziwiri. Ndipo ndinaona mngelo wamphamvu wakulalikira ndi mau akulu, Ayenera ndani kutsegula buku, ndi kumasula zizindikiro zake? Ndipo sanathe mmodzi m'Mwamba, kapena padziko, kapena pansi pa dziko kutsegula pabukupo, kapena kulipenya. Ndipo ndinalira kwambiri, chifukwa sanapezedwa mmodzi woyenera kutsegula bukulo, kapena kulipenya; ndipo mmodzi wa akulu ananena ndi ine, Usalire: taona, Mkango wochokera m'fuko la Yuda, Muzu wa Davide, walakika kutsegula buku ndi zizindikiro zake zisanu ndi ziwiri. Ndipo ndinaona pakati pa mpando wachifumu ndi zamoyo zinai, ndi pakati pa akulu, Mwanawankhosa ali chilili ngati waphedwa; wokhala nazo nyanga zisanu ndi ziwiri, ndi maso asanu ndi awiri, ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu, yotumidwa ilowe m'dziko lonse. Ndipo anadza, nalitenga kudzanja lamanja la Iye wakukhala pa mpando wachifumu. Ndipo pamene adatenga bukulo, zamoyo zinai ndi akulu makumi awiri mphambu anai zinagwa pansi pamaso pa Mwanawankhosa, zonse zili nao azeze, ndi mbale zagolide zodzala ndi zofukiza, ndizo mapemphero a oyera mtima. Ndipo aimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikiro zake; chifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse, ndipo mudawayesa iwo ufumu ndi ansembe kwa Mulungu wathu; ndipo achita ufumu padziko. Ndipo ndinaona, ndipo ndinamva mau a angelo ambiri pozinga mpando wachifumu, ndi zamoyo ndi akulu; ndipo mawerengedwe ao anali zikwi khumi kuchulukitsa zikwi khumi ndi zikwi za zikwi; akunena ndi mau akulu, Ayenera Mwanawankhosa, wophedwayo, kulandira chilimbiko, ndi chuma, ndi nzeru, ndi mphamvu, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi chiyamiko. Ndipo cholengedwa chilichonse chili m'mwamba, ndi padziko, ndi pansi pa dziko, ndi m'nyanja, ndi zonse zili momwemo, ndinazimva zilikunena, Kwa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa zikhale chiyamiko, ndi ulemu, kufikira nthawi za nthawi. Ndipo zamoyo zinai zinati, Amen. Ndipo akuluwo anagwa pansi nalambira. Ndipo ndinaona pamene Mwanawankhosa anamasula chimodzi cha zizindikiro zisanu ndi ziwiri, ndipo ndinamva chimodzi mwa zamoyo zinai, nichinena, ngati mau a bingu, Idza. Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, kavalo woyera, ndipo womkwerayo anali nao uta; ndipo anampatsa korona; ndipo anatulukira wolakika kuti alakike. Ndipo pamene anamasula chizindikiro chachiwiri, ndinamva chamoyo chachiwiri nichinena, Idza. Ndipo anatuluka kavalo wina, wofiira: ndipo anampatsa iye womkwera mphamvu yakuchotsa mtendere pa dziko ndi kuti aphane; ndipo anampatsa iye lupanga lalikulu. Ndipo pamene anamasula chizindikiro chachitatu, ndinamva chamoyo chachitatu nichinena, Idza. Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wakuda; ndipo iye womkwera anali nao muyeso m'dzanja lake. Ndipo ndinamva ngati mau pakati pa zamoyo zinai, nanena, Muyeso wa tirigu wogula rupiya, ndi miyeso itatu ya barele yogula rupiya; ndi mafuta ndi vinyo usaziipse. Ndipo pamene anamasula chizindikiro chachinai, ndinamva mau a chamoyo chachinai nichinena, Idza. Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wotumbuluka; ndipo iye womkwera, dzina lake ndiye Imfa; ndipo dziko la akufa linatsatana naye; ndipo anawapatsa ulamuliro pa dera lachinai la dziko, kukapha ndi lupanga, ndi njala, ndi imfa, ndi zilombo za padziko. Ndipo pamene adamasula chizindikiro chachisanu, ndinaona pansi pa guwa la nsembe mizimu ya iwo adaphedwa chifukwa cha mau a Mulungu, ndi chifukwa cha umboni umene anali nao: ndipo anafuula ndi mau akulu, ndi kunena, Kufikira liti, Mfumu yoyera ndi yoona, muleka kuweruza ndi kubwezera chilango chifukwa cha mwazi wathu, pa iwo akukhala padziko? Ndipo anapatsa yense wa iwo mwinjiro woyera; nanena kwa iwo, kuti apumulebe kanthawi, kufikira atakwaniranso akapolo anzao, ndi abale ao amene adzaphedwa monganso iwo eni. Ndipo ndinaona pamene anamasula chizindikiro chachisanu ndi chimodzi, ndipo panali chivomezi chachikulu; ndi dzuwa lidada bii longa chiguduli cha ubweya ndi mwezi wonse unakhala ngati mwazi; ndi nyenyezi zam'mwamba zinagwa padziko, monga mkuyu utaya nkhuyu zake zosapsa, pogwedezeka ndi mphepo yolimba. Ndipo kumwamba kudachoka monga ngati mpukutu wopindidwa; ndi mapiri onse ndi zisumbu zonse zinatunsidwa kuchoka m'malo mwao. Ndipo mafumu a dziko, ndi akulu, ndi akazembe, ndi achuma, ndi amphamvu, ndi akapolo onse, ndi mfulu, anabisala kumapanga, ndi matanthwe a mapiri; nanena kwa mapiri ndi matanthwe, Igwani pa ife, ndipo tibiseni ife kunkhope ya Iye amene akhala pa mpando wachifumu, ndi kumkwiyo wa Mwanawankhosa; chifukwa lafika tsiku lalikulu la mkwiyo wao, ndipo akhoza kuima ndani? Zitatha izi ndinaona angelo anai alinkuimirira pangodya zinai za dziko, akugwira mphepo zinai za dziko, kuti ingaombe mphepo padziko, kapena panyanja, kapena pa mtengo uliwonse. Ndipo ndinaona mngelo wina, anakwera kuchokera potuluka dzuwa, ali nacho chizindikiro cha Mulungu wamoyo: ndipo anafuula ndi mau akulu kuitana angelo anai, amene adalandira mphamvu kuipsa dziko ndi nyanja, nanena, Musaipse dziko, kapena nyanja, kapena mitengo, kufikira tidasindikiza chizindikiro akapolo a Mulungu wathu, pamphumi pao. Ndipo ndinamva chiwerengo cha iwo osindikizidwa chizindikiro, zikwi makumi khumi ndi makumi anai mphambu anai, osindikizidwa chizindikiro mwa mafuko onse a ana a Israele. Mwa fuko la Yuda anasindikizidwa chizindikiro zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Rubeni zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Gadi zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Asere zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Nafutali zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Manase zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Simeoni zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko Levi zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Isakara zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Zebuloni zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Yosefe zikwi khumi ndi ziwiri. Mwa fuko la Benjamini anasindikizidwa chizindikiro zikwi khumi ndi ziwiri. Zitatha izi ndinapenya, taonani, khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliwerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, akuimirira kumpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atavala zovala zoyera, ndi makhwatha a kanjedza m'manja mwao; ndipo afuula ndi mau akulu, nanena, Chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa. Ndipo angelo onse anaimirira pozinga mpando wachifumu, ndi akulu, ndi zamoyozo zinai; ndipo anagwa nkhope yao pansi kumpando wachifumu, nalambira Mulungu, ndi kunena, Amen: Thamo ndi ulemerero, ndi nzeru, ndi chiyamiko, ndi ulemu, ndi chilimbiko, ndi mphamvu zikhale kwa Mulungu wathu kufikira nthawi za nthawi. Amen. Ndipo mmodzi wa akulu anayankha, nanena ndi ine, Iwo ovala zovala zoyera ndiwo ayani, ndipo achokera kuti? Ndipo ndinati kwa iye, Mbuye wanga, mudziwa ndinu. Ndipo anati kwa ine, Iwo ndiwo akutuluka m'chisautso chachikulu; ndipo anatsuka zovala zao, naziyeretsa m'mwazi wa Mwanawankhosa. Chifukwa chake ali kumpando wachifumu wa Mulungu; ndipo amtumikira Iye usana ndi usiku m'Kachisi mwake; ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu adzawachitira mthunzi, sadzamvanso njala, kapena ludzu, kapena silidzawatentha dzuwa, kapena chitungu chilichonse; chifukwa Mwanawankhosa wakukhala pakati pa mpando wachifumu adzawaweta, nadzawatsogolera ku akasupe a madzi amoyo, ndipo Mulungu adzawapukutira misozi yonse pamaso pao. Ndipo pamene anamasula chizindikiro chachisanu ndi chiwiri, munali chete m'Mwamba monga mwa nthawi ya ora latheka. Ndipo ndinaona angelo asanu ndi awiri amene amaimirira pamaso pa Mulungu; ndipo anawapatsa malipenga asanu ndi awiri. Ndipo anadza mngelo wina, naima pa guwa la nsembe, nakhala nacho chotengera cha zofukiza chagolide; ndipo anampatsa zofukiza zambiri, kuti aziike pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima onse pa guwa la nsembe lagolide, lokhala kumpando wachifumu. Ndipo utsi wa zofukiza, pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima unakwera kutuluka m'dzanja la mngelo, pamaso pa Mulungu. Ndipo mngeloyo anatenga mbale ya zofukiza, naidzaza ndi moto wopala pa guwa la nsembe, nauponya pa dziko lapansi; ndipo panakhala mabingu, ndi mau, ndi mphezi, ndi chivomezi. Ndipo angelo asanu ndi awiri akukhala nao malipenga anadzikonzera kuti aombe. Ndipo woyamba anaomba lipenga, ndipo panakhala matalala ndi moto, zosanganiza ndi mwazi, ndipo anazitaya pa dziko lapansi; ndipo limodzi la magawo atatu a dziko lidapserera, ndipo limodzi la magawo atatu a mitengo lidapserera, ndipo msipu wonse udapserera. Ndipo mngelo wachiwiri anaomba lipenga, ndipo monga ngati phiri lalikulu lakupserera ndi moto linaponyedwa m'nyanja; ndipo limodzi la magawo atatu a nyanja linasanduka mwazi; ndipo lidafa limodzi la magawo atatu a zolengedwa zili m'nyanja, zokhala ndi moyo; ndipo limodzi la magawo atatu a zombo lidaonongeka. Ndipo mngelo wachitatu anaomba lipenga, ndipo idagwa kuchokera kumwamba nyenyezi yaikulu, yoyaka ngati muuni, ndipo idagwa pa limodzi la magawo atatu a mitsinje, ndi pa akasupe amadzi; ndipo dzina lake la nyenyeziwo alitcha Chowawa; ndipo limodzi la magawo atatu a madzi lidasanduka chowawa; ndipo anthu ambiri adafa pakumwa madzi, pakuti asananduka owawa. Ndipo mngelo wachinai anaomba lipenga, ndipo limodzi la magawo atatu a dzuwa linagwidwa, ndi limodzi la magawo atatu a mwezi, ndi limodzi la magawo atatu a nyenyezi; kuti limodzi la magawo ao atatu lidetsedwe, ndi kuti limodzi la magawo ake atatu a usana lisawale, ndi usiku momwemo. Ndipo ndinaona, ndipo ndinamva chiombankhanga chilikuuluka pakati pa mwamba, ndi kunena ndi mau akulu, Tsoka, tsoka, tsoka, iwo akukhala padziko, chifukwa cha mau otsala a lipenga la angelo atatu asanaombe. Ndipo mngelo wachisanu anaomba lipenga, ndipo ndinaona nyenyezi yochokera kumwamba idagwa padziko; ndipo anampatsa iye chifunguliro cha chiphompho chakuya. Ndipo anatsegula pa chiphompho chakuya; ndipo unakwera utsi wotuluka m'chiphomphomo, ngati utsi wa ng'anjo yaikulu; ndipo dzuwa ndi thambo zinada, chifukwa cha utsiwo wa kuchiphomphocho. Ndipo m'utsimo mudatuluka dzombe padziko, ndipo analipatsa ilo mphamvu monga zinkhanira za dziko zili ndi mphamvu. Ndipo ananena kwa ilo kuti lisaipse udzu wa padziko, kapena chabiriwiri chilichonse, kapena mtengo uliwonse, koma anthu amene alibe chizindikiro cha Mulungu pamphumi pao ndiwo. Ndipo anapatsa ilo mphamvu si kuti likawaphe, komatu kuti likawazunze miyezi isanu; ndipo mazunzidwe ao anali ngati mazunzidwe a chinkhanira, pamene chiluma munthu. Ndipo m'masiku ajawo, anthu adzafunafuna imfa osaipeza konse; ndipo adzakhumba kumwalira, koma imfa idzawathawa. Ndipo maonekedwe a dzombelo anafanana ndi akavalo okonzeka kukachita nkhondo; ndi pamitu pao ngati akorona onga agolide, ndi pankhope pao ngati pankhope pa anthu. Ndipo anali nalo tsitsi longa tsitsi la akazi, ndipo mano ao anali ngati mano a mikango. Ndipo anali nazo zikopa ngati zikopa zachitsulo; ndipo mkokomo wa mapiko ao ngati mkokomo wa agaleta, a akavalo ambiri akuthamangira kunkhondo. Ndipo lili nayo michira yofanana ndi ya chinkhanira ndi mbola; ndipo m'michira mwao muli mphamvu yao yakuipsa anthu miyezi isanu. Ndipo linali nayo Mfumu yakulilamulira, mngelo wa chiphompho chakuya; dzina lake m'Chihebri Abadoni, ndi m'Chigriki ali nalo dzina Apoliyoni. Tsoka loyamba lapita; taonani, akudzanso matsoka awiri m'tsogolomo. Ndipo mngelo wachisanu ndi chimodzi anaomba lipenga, ndipo ndinamva mau ochokera kunyanga za guwa la nsembe lagolide lili pamaso pa Mulungu, nanena kwa mngelo wachisanu ndi chimodzi wakukhala ndi lipenga, Masula angelo anai omangidwa pa mtsinje waukulu Yufurate. Ndipo anamasulidwa angelo anai, okonzeka kufikira ora ndi tsiku ndi mwezi ndi chaka, kuti akaphe limodzi la magawo atatu a anthu. Ndipo chiwerengero cha nkhondo za apakavalo ndicho zikwi makumi awiri zochulukitsa zikwi khumi; ndinamva chiwerengero chao. Ndipo kotero ndinaona akavalo m'masomphenya, ndi iwo akuwakwera akukhala nazo zikopa za moto, ndi huakinto ndi sulufure; ndi mitu ya akavalo ngati mitu ya mikango; ndipo m'kamwa mwao mutuluka moto ndi utsi ndi sulufure. Ndi miliri iyi linaphedwa limodzi la magawo atatu a anthu, ndi moto, ndi utsi, ndi sulufure, zotuluka m'kamwa mwao. Pakuti mphamvu ya akavalo ili m'kamwa mwao, ndi m'michira yao; pakuti michira yao ifanana ndi njoka, nikhala nayo mitu, ndipo aipsa nayoyo. Ndipo otsala a anthu osaphedwa nayo miliri iyo sanalapa ntchito ya manja ao, kuti asapembedzere ziwanda, ndi mafano agolide, ndi asiliva, ndi amkuwa, ndi a mwala, ndi amtengo, amene sakhoza kupenya, kapena kumva, kapena kuyenda; ndipo sanalapa mbanda zao, kapena nyanga zao, kapena chigololo chao, kapena umbala wao. Ndipo ndinaona mngelo wina wolimba alikutsika Kumwamba, wovala mtambo; ndi utawaleza pamutu pake, ndi nkhope yake ngati dzuwa, ndi mapazi ake ngati mizati yamoto; ndipo anali nako m'dzanja lake kabuku kofunyulula: ndipo anaponda nalo phazi lake lamanja panyanja, ndi lamanzerelo pamtunda, nafuula ndi mau akulu, monga ngati mkango ubangula; ndipo pamene anafuula mabingu asanu ndi awiri analankhula mau ao. Ndipo pamene adalankhula mabingu asanu ndi awiriwo, ndinati ndilembe; ndipo ndinamva mau ochokera Kumwamba nanena, Sindikiza nacho chizindikiro zimene adalankhula mabingu asanu ndi awiri, ndipo usazilembe. Ndipo mngelo amene ndinamuona alikuimirira panyanja ndi pa mtunda, anakweza dzanja lake lamanja kuloza kumwamba, nalumbira kutchula Iye amene ali ndi moyo kunthawi za nthawi, amene analenga m'mwamba ndi zinthu zili momwemo, ndi dziko lapansi ndi zinthu zili momwemo, ndi nyanja ndi zinthu zili momwemo kuti sipadzakhalanso nthawi: komatu m'masiku a mau a mngelo wachisanu ndi chiwiri m'mene iye adzayamba kuomba lipenga, pamenepo padzatsirizika chinsinsi cha Mulungu, monga analalikira kwa akapolo ake aneneri. Ndipo mau ndinawamva ochokera Kumwamba, analankhulanso nane, nanena, Muka, tenga buku lofunyululalo m'dzanja la mngelo wakuimirira panyanja ndi padziko. Ndipo ndinamuka kwa mngelo, ndi kunena naye, Ndipatse kabukuko. Ndipo ananena ndi ine, Dzatenge, nudye; ndipo kadzawawitsa m'mimba mwako, komatu m'kamwa mwako kadzazuna ngati uchi. Ndipo ndinatenga kabuku m'dzanja la mngelo, ndipo ndinakadya; ndipo kanali m'kamwa mwanga kozuna ngati uchi; ndipo pamene ndinakadya m'mimba mwanga mudawawa. Ndipo ananena nane, Uyenera iwe kuneneranso pa anthu ndi mitundu, ndi manenedwe, ndi mafumu ambiri. Ndipo anandipatsa ine bango ngati ndodo, ndi kuti, Tanyamuka, nuyese Kachisi wa Mulungu, ndi guwa la nsembe, ndi iwo akulambiramo. Ndipo bwalo la kunja kwa Kachisi ulisiye padera, osaliyesa; pakuti adapatsa ilo kwa amitundu; ndipo mzinda wopatulika adzaupondereza miyezi makumi anai mphambu iwiri. Ndipo ndidzalamulira mboni zanga ziwiri, ndipo zidzanenera masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri amphambu makumi asanu ndi limodzi, zovala chiguduli. Izo ndizo mitengo iwiri ya azitona ndi zoikapo nyali ziwiri zakuima pamaso pa Ambuye wa dziko lapansi. Ndipo wina akafuna kuipsa izo, moto utuluka m'kamwa mwao, nuononga adani ao; ndipo wina akafuna kuipsa izo, maphedwe ake ayenera kutero. Izo zili nao ulamuliro wakutseka m'mwamba, isagwe mvula masiku a chinenero chao; ndipo ulamuliro zili nao pamadzi kuwasandutsa mwazi, ndi kupanda dziko ndi mliri uliwonse nthawi iliyonse zikafuna. Ndipo pamene zidatsiriza umboni wao chilombo chokwera kutuluka m'chiphompho chakuya chidzachita nazo nkhondo, nichidzazilaka, nichidzazipha izo. Ndipo mitembo yao idzakhala pa khwalala lamudzi waukulu, umene utchedwa, ponena zachizimu, Sodomu ndi Ejipito, pameneponso Ambuye wao anapachikidwa. Ndipo a mwa anthu ndi mafuko, ndi manenedwe, ndi mitundu apenyera mitembo yao masiku atatu ndi nusu lake, osalola mitembo yao iikidwe m'manda. Ndipo iwo akukhala padziko adzakondwerera, nasekerera, nadzatumizirana mitulo; popeza aneneri awa awiri anazunza iwo akukhala padziko. Ndipo atapita masiku atatu ndi nusu lake mzimu wamoyo wochokera kwa Mulungu unawalowera, ndipo anakhala chilili; ndipo mantha akulu anawagwera iwo akuwapenya. Ndipo anamva mau akulu akuchokera Kumwamba akunena nao, Kwerani kuno. Ndipo anakwera kunka Kumwamba mumtambo; ndipo adani ao anawapenya. Ndipo panthawipo panali chivomezi chachikulu, ndipo limodzi la magawo khumi a mudzi lidagwa; ndipo anaphedwa m'chivomezicho anthu zikwi zisanu ndi ziwiri; ndipo otsalawo anakhala amantha, napatsa ulemerero kwa Mulungu wa m'Mwamba. Tsoka lachiwiri lachoka; taonani, tsoka lachitatu lidza msanga. Ndipo mngelo wachisanu ndi chiwiri anaomba lipenga, ndipo panakhala mau akulu m'Mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Khristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi. Ndipo akulu makumi awiri mphambu anai akukhala pamaso pa Mulungu pa mipando yachifumu yao, anagwa nkhope yao pansi nalambira Mulungu, nati, Tikuyamikani, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse, amene muli, nimunali; popeza mwadzitengera mphamvu yanu yaikulu, ndipo mwachita ufumu. Ndipo amitundu anakwiya, ndipo unadza mkwiyo wanu, ndi nthawi ya akufa yakuti aweruzidwe, ndi yakupereka mphotho akapolo anu aneneriwo, ndi oyera mtima, ndi iwo akuopa dzina lanu, ang'ono ndi akulu; ndi kuononga iwo akuononga dziko. Ndipo anatsegulidwa Kachisi wa Mulungu amene ali m'Mwamba; ndipo linaoneka likasa la chipangano chake, m'Kachisi mwake, ndipo panali mphezi, ndi mau, ndi mabingu, ndi chivomezi, ndi matalala akulu. Ndipo chizindikiro chachikulu chinaoneka m'mwamba; mkazi wovekedwa dzuwa, ndi mwezi kumapazi ake, ndi pamutu pake korona wa nyenyezi khumi ndi ziwiri; ndipo anali ndi pakati; ndipo afuula alimkubala, ndi kumva zowawa zakubala. Ndipo chinaoneka chizindikiro china m'mwamba taonani, chinjoka chofiira, chachikulu, chakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri, ndi nyanga khumi, ndi pamutu pake nduwira zachifumu zisanu ndi ziwiri. Ndipo mchira wake uguza limodzi la magawo atatu a nyenyezi zam'mwamba, nuziponya padziko. Ndipo chinjoka chinaimirira pamaso pa mkazi akuti abale, kuti, akabala icho chikalikwire mwana wake. Ndipo anabala mwana wamwamuna, amene adzaweruza mitundu yonse ndi ndodo yachitsulo: ndipo anakwatulidwa mwana wake amuke kwa Mulungu, ndi kumpando wachifumu wake. Ndipo mkazi anathawira kuchipululu, kumene ali nayo mbuto yokonzekeratu ndi Mulungu, kuti kumeneko akamdyetse masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi. Ndipo munali nkhondo m'mwamba. Mikaele ndi angelo ake akuchita nkhondo ndi chinjoka; chinjokanso ndi angelo ake chinachita nkhondo; ndipo sichinalakika, ndipo sanapezekanso malo ao m'mwamba. Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdierekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi. Ndipo ndinamva mau akulu m'Mwamba, nanena, Tsopano zafika chipulumutso, ndi mphamvu, ndi ufumu za Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Khristu wake; pakuti wagwetsedwa wonenera wa abale athu, wakuwanenera pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku. Ndipo iwo anamlaka iye chifukwa cha mwazi wa Mwanawankhosa, ndi chifukwa cha mau a umboni wao; ndipo sanakonda moyo wao kungakhale kufikira imfa. Chifukwa chake, kondwerani, miyamba inu, ndi inu akukhala momwemo. Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa mdierekezi watsikira kwa inu, wokhala nao udani waukulu, podziwa kuti kamtsalira kanthawi. Ndipo pamene chinjoka chinaona kuti chinaponyedwa pansi kudziko, chinazunza mkazi amene adabala mwana wamwamuna. Ndipo anapatsa mkazi mapiko awiri a chiombankhanga chachikulu, kuti akaulukire kuchipululu, ku mbuto yake, kumene adyetsedwako nthawi, ndi zinthawi, ndi nusu la nthawi, osapenya nkhope ya njoka. Ndipo njokayo inalavula m'kamwa mwake, madzi ngati mtsinje, potsata mkazi, kuti mkaziyo akakokoleredwe nao. Ndipo dziko linathandiza mkaziyo, ndi dziko linatsegula m'kamwa mwake, nilinameza madzi a mtsinje amene chinjoka chinalavula m'kamwa mwake. Ndipo chinjoka chinakwiya ndi mkazi, nichinachoka kunka kuchita nkhondo ndi otsala a mbeu yake, amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nao umboni wa Yesu. Ndipo chinjokacho chinakaimirira m'mbali mwa nyanja. Ndipo ndinaimirira pa mchenga wa nyanja. Ndipo ndinaona chilombo chilinkutuluka m'nyanja, chakukhala nazo nyanga khumi, ndi mitu isanu ndi iwiri, ndi pa nyanga zake nduwira zachifumu khumi, ndi pamitu pake maina a mwano. Ndipo chilombo ndinachionacho chinafanana ndi nyalugwe, ndi mapazi ake ngati mapazi a chimbalangondo, ndi pakamwa pake ngati pakamwa pa mkango; ndipo chinjoka chinampatsa iye mphamvu yake, ndi mpando wachifumu wake, ndi ulamuliro waukulu. Ndipo umodzi wa mitu yake unakhala ngati unalasidwa kufikira imfa; ndipo bala lake la kuimfa lidapola; ndipo dziko lonse linazizwa potsata chilombocho; ndipo analambira chinjoka, chifukwa chinachipatsa ulamuliro chilombocho; ndipo analambira chilombo ndi kunena, Afanana ndi chilombo ndani? Ndipo akhoza ndani kugwira nkhondo nacho? Ndipo anachipatsa icho m'kamwa molankhula zazikulu ndi zamwano; ndipo anachipatsa ulamuliro wa kutero miyezi makumi anai ndi iwiri. Ndipo chinatsegula pakamwa pake kukanena zamwano pa Mulungu, kuchitira mwano dzina lake, ndi chihema chake, ndi iwo akukhala m'Mwamba. Ndipo anachipatsa icho kuchita nkhondo ndi oyera mtima, ndi kuwalaka; ndipo anachipatsa ulamuliro wa pa fuko lililonse, ndi anthu, ndi manenedwe, ndi mitundu. Ndipo adzachilambira onse akukhala padziko, amene dzina lao silinalembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa, wophedwa kuyambira makhazikidwe a dziko lapansi. Ngati wina ali nalo khutu, amve. Ngati munthu alinga kundende, kundende adzamuka; munthu akapha ndi lupanga, ayenera iye kuphedwa nalo lupanga. Pano pali chipiriro ndi chikhulupiriro cha oyera mtima. Ndipo ndinaona chilombo china chilikutuluka pansi; ndipo chinali nazo nyanga ziwiri ngati za mwanawankhosa, ndipo chinalankhula ngati chinjoka. Ndipo chichita ulamuliro wonse wa chilombo choyamba pamaso pake. Ndipo chilambiritsa dziko ndi iwo akukhala momwemo chilombo choyamba, chimene bala lake la kuimfa lidapola. Ndipo chichita zizindikiro zazikulu, kutinso chitsitse moto uchokere m'mwamba nugwe padziko, pamaso pa anthu. Ndipo chisokeretsa iwo akukhala padziko ndi zizindikiro zimene anachipatsa mphamvu yakuzichita pamaso pa chilombo, ndi kunena kwa iwo akukhala padziko, kuti apange fano la chilombocho, chimene chinali nalo bala la lupanga nichinakhalanso ndi moyo. Ndipo anachipatsa mphamvu yakupatsa fano la chilombo mpweya, kutinso fano la chilombo lilankhule, nilichite kuti onse osalilambira fano la chilombo aphedwe. Ndipo chichita kuti onse, ang'ono ndi akulu, achuma ndi osauka, ndi mfulu ndi akapolo, alandire chilembo pa dzanja lao ndi pamphumi pao; ndi kuti munthu sangakhoze kugula kapena kugulitsa, koma iye yekha wakukhala nacho chilembo, ndilo dzina la chilombo, kapena chiwerengero cha dzina lake. Pano pali nzeru. Iye wakukhala nacho chidziwitso awerenge chiwerengero cha chilombocho; pakuti chiwerengero chake ndi cha munthu; ndipo chiwerengero chake ndicho mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu ndi chimodzi. Ndipo ndinapenya, taonani, Mwanawankhosayo alikuimirira pa phiri la Ziyoni, ndipo pamodzi ndi Iye zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, akukhala nalo dzina lake ndi dzina la Atate wake lolembedwa pamphumi pao. Ndipo ndinamva mau ochokera Kumwamba, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ndi ngati mau a bingu lalikulu; ndipo mau amene ndinawamva anakhala ngati a azeze akuimba azeze ao; ndipo aimba ngati nyimbo yatsopano kumpando wachifumu, ndi pamaso pa zamoyo zinai, ndi akulu; ndipo palibe munthu anakhoza kuphunzira nyimboyi, koma zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, ogulidwa kuchokera kudziko. Iwo ndiwo amene sadetsedwa pamodzi ndi akazi; pakuti ali anamwali. Iwo ndiwo amene atsata Mwanawankhosa kulikonse amukako. Iwowa anagulidwa mwa anthu, zipatso zoundukula kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa. Ndipo m'kamwa mwao simunapezedwa bodza; ali opanda chilema. Ndipo ndinaona mngelo wina alikuuluka pakati pa mlengalenga, wakukhala nao Uthenga Wabwino wosatha, aulalikire kwa iwo akukhala padziko, ndi kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu; ndi kunena ndi mau akulu, Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthawi ya chiweruziro chake; ndipo mlambireni Iye amene analenga m'mwamba ndi mtunda ndi nyanja ndi akasupe amadzi. Ndipo anatsata mngelo wina mnzake ndi kunena, Wagwa, wagwa, Babiloni waukulu umene unamwetsako mitundu yonse ku vinyo wa mkwiyo wa chigololo chake. Ndipo anawatsata mngelo wina, wachitatu, nanena ndi mau akulu, Ngati wina alambira chilombocho, ndi fano lake, nalandira lemba pamphumi pake, kapena pa dzanja lake iyenso adzamwako kuvinyo wa mkwiyo wa Mulungu, wokonzeka wosasanganiza m'chikho cha mkwiyo wake; ndipo adzazunzika ndi moto ndi sulufure pamaso pa angelo oyera mtima ndi pamaso pa Mwanawankhosa; ndipo utsi wa kuzunza kwao ukwera kunthawi za nthawi; ndipo sapuma usana ndi usiku iwo akulambira chilombocho ndi fano lake, ndi iye aliyense akalandira lemba la dzina lake. Pano pali chipiriro cha oyera mtima, cha iwo akusunga malamulo a Mulungu, ndi chikhulupiriro cha Yesu. Ndipo ndinamva mau ochokera Kumwamba, ndi kunena, Lemba, Odala akufa akumwalira mwa Ambuye, kuyambira tsopano; inde, anena Mzimu, kuti akapumule ku zolemetsa zao; pakuti ntchito zao zitsatana nao pamodzi. Ndipo ndinapenya, taonani, mtambo woyera; ndi pamtambo padakhala wina monga Mwana wa Munthu, wakukhala naye korona wagolide pamutu pake, ndi m'dzanja lake chisenga lakuthwa. Ndipo mngelo wina anatuluka m'Kachisi, wofuula ndi mau akulu kwa Iye wakukhala pamtambo, Tumiza chisenga chako ndi kumweta, pakuti yafika nthawi yakumweta; popeza dzinthu za dziko zachetsa. Ndipo Iye wokhala pamtambo anaponya chisenga chake padziko, ndipo dzinthu za dziko zinamwetedwa. Ndipo mngelo wina anatuluka m'Kachisi ali m'Mwamba, nakhala nacho chisenga chakuthwa nayenso. Ndipo mngelo wina anatuluka pa guwa la nsembe, ndiye wakukhala nao ulamuliro pamoto; nafuula ndi mau akulu kwa iye wakukhala nacho chisenga chakuthwa, nanena, Tumiza chisenga chako chakuthwa, nudule matsango a munda wampesa wa m'dziko; pakuti mphesa zake zapsa ndithu. Ndipo mngelo anaponya chisenga chake kudziko nadula mphesa za m'munda wa m'dziko, naziponya moponderamo mphesa mwamukulu mwa mkwiyo wa Mulungu. Ndipo moponderamo mphesa anamuponda kunja kwa mudzi, ndipo mudatuluka mwazi moponderamo mphesa, kufikira zapakamwa za akavalo, kufikira mastadiya chikwi ndi mazana asanu ndi limodzi. Ndipo ndinaona chizindikiro china m'mwamba, chachikulu ndi chozizwitsa, angelo asanu ndi awiri akukhala nayo miliri isanu ndi iwiri, ndiyo yotsiriza, kuti mwa iyo watsirizika mkwiyo wa Mulungu. Ndipo ndinaona ngati nyanja yagalasi yosanganiza ndi moto; ndipo iwo amene anachilaka chilombocho, ndi fano lake ndi chiwerengero cha dzina lake, anaimirira pa nyanja yagalasi, nakhala nao azeze a Mulungu. Ndipo aimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa, nanena, Ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu Inu ya nthawi zosatha. Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Chifukwa Inu nokha muli woyera; chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa. Ndipo zitatha izi ndinaona, ndipo panatseguka pa Kachisi wa chihema cha umboni m'Mwamba: ndipo anatuluka m'Kachisi angelo asanu ndi awiri akukhala nayo miliri isanu ndi iwiri, atavala malaya woyera, ndi wonyezimira, namangira malamba agolide pachifuwa pao. Ndipo chimodzi cha zamoyo zinai chinapatsa angelo asanu ndi awiri mbale zisanu ndi ziwiri zagolide zodzala ndi mkwiyo wa Mulungu wakukhala ndi moyo ku nthawi za nthawi. Ndipo Kachisi anadzazidwa ndi utsi wochokera ku ulemerero wa Mulungu ndi ku mphamvu yake; ndipo palibe munthu anakhoza kulowa m'Kachisi kufikira ikatha miliri isanu ndi iwiri ya angelo asanu ndi awiri. Ndipo ndinamva mau akulu ochokera ku Kachisi, akunena kwa angelo asanu ndi awiri, Mukani, ndipo tsanulirani kudziko mbale zisanu ndi ziwiri za mkwiyo wa Mulungu. Ndipo anachoka woyamba, natsanulira mbale yake kudziko; ndipo kunakhala chilonda choipa ndi chosautsa pa anthu akukhala nalo lemba la chilombo nalambira fano lake. Ndipo wachiwiri anatsanulira mbale yake m'nyanja; ndipo kunakhala mwazi ngati wa munthu wakufa; ndipo zamoyo zonse za m'nyanja zidafa. Ndipo wachitatu anatsanulira mbale yake kumitsinje ndi akasupe a madzi; ndipo kunasanduka mwazi. Ndipo ndinamva mngelo wa madziwo nanena, Muli wolungama, amene muli, nimunali, Woyera Inu, chifukwa mudaweruza kotero; popeza anatsanulira mwazi wa oyera mtima, ndi wa aneneri, ndipo mudawapatsa mwazi amwe; ayenera iwo. Ndipo ndinamva wa pa guwa la nsembe, alinkunena, Inde, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse, maweruziro anu ali oona ndi olungama. Ndipo wachinai anatsanulira mbale yake padzuwa; ndipo analipatsa ilo litenthe anthu ndi moto. Ndipo anatenthedwa anthu ndi kutentha kwakukulu; ndipo anachitira mwano dzina la Mulungu wokhala nao ulamuliro pa miliri iyi; ndipo sanalapa kuti amchitire ulemu. Ndipo wachisanu anatsanulira mbale yake pa mpando wachifumu wa chilombo; ndipo ufumu wake unadetsedwa; ndipo anatafuna malilime ao ndi kuwawa kwake, nachitira mwano Mulungu wa m'Mwamba chifukwa cha zowawa zao ndi zilonda zao; ndipo sanalapa ntchito zao. Ndipo wachisanu ndi chimodzi anatsanulira mbale yake pa mtsinje waukulu Yufurate; ndi madzi ake anaphwa, kuti ikonzeke njira ya mafumu ochokera potuluka dzuwa. Ndipo ndinaona motuluka m'kamwa mwa chinjoka, ndi m'kamwa mwa chilombo, ndi m'kamwa mwa mneneri wonyenga mizimu itatu yonyansa, ngati achule; pakuti ali mizimu ya ziwanda zakuchita zizindikiro; zimene zituluka kunka kwa mafumu a dziko lonse, kuwasonkhanitsira kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse. (Taonani, ndidza ngati mbala. Wodala iye amene adikira, nasunga zovala zake, kuti angayende wausiwa, nangapenye anthu usiwa wake.) Ndipo anawasonkhanitsira kumalo otchedwa m'Chihebri Armagedoni. Ndipo wachisanu ndi chiwiri anatsanulira mbale yake mumlengalenga; ndipo m'Kachisimo mudatuluka mau akulu, ochokera kumpando wachifumu ndi kunena, Chachitika; ndipo panakhala mphezi, ndi mau, ndi mabingu; ndipo panali chivomezi chachikulu chotero sichinaoneke chiyambire anthu padziko, chivomezi cholimba chotero, chachikulu chotero. Ndipo chimudzi chachikulucho chidagawika patatu, ndi midzi ya amitundu inagwa; ndipo Babiloni waukulu unakumbukika pamaso pa Mulungu, kuti aupatse chikho cha vinyo wamkali wa mkwiyo wake. Ndipo zisumbu zonse zidathawa, ndi mapiri sanapezeka. Ndipo anatsika kumwamba matalala akulu, lonse lolemera ngati talente, nagwa pa anthu; ndipo anthu anachitira Mulungu mwano chifukwa cha mliri wa matalala, pakuti mliri wake ndi waukulu ndithu. Ndipo anadza mmodzi mwa angelo asanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, nalankhula ndi ine, nanena, Idza kuno, ndidzakuonetsa chitsutso cha mkazi wachigololo wamkulu, wakukhala pa madzi ambiri, amene mafumu a dziko anachita chigololo naye, ndipo iwo akukhala padziko analedzera ndi vinyo wa chigololo chake. Ndipo ananditenga kunka nane kuchipululu, mu Mzimu; ndipo ndinaona mkazi alinkukhala pachilombo chofiira, chodzala ndi maina a mwano, chakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi. Ndipo mkazi anavala chibakuwa, ndi mlangali, nakometsedwa ndi golide, ndi miyala ya mtengo wake, ndi ngale; nakhala nacho m'dzanja lake chikho chagolide chodzala ndi zonyansitsa, ndi zodetsa za chigololo chake, ndipo pamphumi pake padalembedwa dzina, CHINSINSI, BABILONI WAUKULU, AMAI WA ACHIGOLOLO NDI WA ZONYANSITSA ZA DZIKO. Ndipo ndinaona mkazi woledzera ndi mwazi wa oyera mtima, ndi mwazi wa mboni za Yesu; ndipo ndinazizwa pakumuona iye ndi kuzizwa kwakukulu. Ndipo mngelo anati kwa ine, Uzizwa chifukwa ninji? Ine ndidzakuuza iwe chinsinsi cha mkazi, ndi cha chilombo chakumbereka iye, chokhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi. Chilombo chimene unachiona chinaliko, koma kulibe; ndipo chidzatuluka m'chiphompho chakuya, ndi kunka kuchitayiko. Ndipo adzazizwa iwo akukhala padziko amene dzina lao silinalembedwa m'buku la moyo chiyambire makhazikidwe a dziko lapansi, pakuona chilombo, kuti chinaliko, ndipo kulibe, ndipo chidzakhalako. Pano pali mtima wakukhala nayo nzeru. Mitu isanu ndi iwiri ndiyo mapiri asanu ndi awiri amene mkazi akhalapo; ndipo ali mafumu asanu ndi awiri asanu adagwa, imodzi iliko, yinayo siinadze; ndipo pamene ifika iyenera iyo kukhala kanthawi. Ndipo chilombo chinalicho, ndi kulibe, icho chomwe ndicho chachisanu ndi chitatu, ndipo chili mwa zisanu ndi ziwirizo, nichimuka kuchitayiko. Ndipo nyanga khumi udaziona ndiwo mafumu khumi, amene sanalandire ufumu; koma alandira ulamuliro ngati mafumu, ora limodzi, pamodzi ndi chilombo. Iwo ali nao mtima umodzi, ndipo apereka mphamvu ndi ulamuliro wao kwa chilombo. Iwo adzachita nkhondo pa Mwanawankhosa, ndipo Mwanawankhosa adzawalaka, chifukwa ali Mbuye wa ambuye, ndi Mfumu ya mafumu; ndipo adzawalakanso iwo akukhala naye, oitanidwa, ndi osankhika ndi okhulupirika. Ndipo anena ndi ine, Madziwo udawaona uko akhalako mkazi wachigololoyo ndiwo anthu, ndi makamu, ndi mitundu, ndi manenedwe. Ndipo nyanga khumi udaziona, ndi chilombo, izi zidzadana ndi mkazi wachigololoyo, nizidzamkhalitsa wabwinja wausiwa, nizidzadya nyama yake, nizidzampsereza ndi moto. Pakuti Mulungu anapatsa kumtima kwao kuchita za m'mtima mwake, ndi kuchita cha mtima umodzi ndi kupatsa ufumu wao kwa chilombo, kufikira akwaniridwa mau a Mulungu. Ndipo mkaziyo unamuona, ndiye mudzi waukulu, wakuchita ufumu pa mafumu a dziko. Zitatha izi ndinaona mngelo wina wakutsika m'Mwamba wakukhala nao ulamuliro waukulu; ndipo dziko linaunikidwa ndi ulemerero wake. Ndipo anafuula ndi mau olimba, nanena, Wagwa, wagwa, Babiloni waukulu, nusandulika mokhalamo ziwanda, ndi mosungiramo mizimu yonse yonyansa, ndi mosungiramo mbalame zonse zonyansa ndi zodanidwa. Chifukwa ndi vinyo wa mkwiyo wa chigololo chake mitundu yonse idagwa; ndipo mafumu a dziko anachita naye chigololo; ndipo ochita malonda a dziko analemera ndi mphamvu ya kudyerera kwake. Ndipo ndinamva mau ena ochokera Kumwamba, nanena, Tulukani m'menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake; pakuti machimo ake anaunjikizana kufikira m'Mwamba, ndipo Mulungu anakumbuka zosalungama zake. Muubwezere, monganso uwu unabwezera, ndipo muwirikize kawiri, monga mwa ntchito zake; m'chikhomo unathiramo, muuthirire chowirikiza. Monga momwe unadzichitira ulemu, nudyerera, momwemo muuchitire chouzunza ndi chouliritsa maliro: pakuti unena mumtima mwake, Ndikhala ine mfumu, wosati wamasiye ine, wosaona maliro konse ine. Chifukwa chake miliri yake idzadza m'tsiku limodzi, imfa, ndi maliro, ndi njala; ndipo udzapserera ndi moto; chifukwa Ambuye Mulungu wouweruza ndiye wolimba. Ndipo mafumu a dziko ochita chigololo nadyerera naye, adzalira nadzaulira maliro pamene aona utsi wa kutentha kwake, poima patali, chifukwa chakuopa chizunzo chake, nanena, Tsoka, tsoka, mudzi waukuluwo, Babiloni, mudzi wolimba! Pakuti m'ora limodzi chafika chiweruziro chanu. Ndipo ochita malonda a m'dziko adzalira nadzauchitira chifundo, popeza palibe munthu agulanso malonda ao; malonda a golide, ndi a siliva, ndi a mwala wa mtengo wake, ndi a ngale, ndi a nsalu yabafuta, ndi a chibakuwa, ndi a yonyezimira, ndi a mlangali; ndi mitengo yonse ya fungo lokoma, ndi chotengera chilichonse cha minyanga ya njovu, ndi chotengera chilichonse chamtengo wa mtengo wake wapatali, ndi chamkuwa ndi chachitsulo, ndi chansangalabwi; ndi sinamoni ndi amomo, ndi zofukiza, ndi mure, ndi lubani, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi ufa wosalala, ndi tirigu, ndi ng'ombe, ndi nkhosa; ndi malonda a akavalo, ndi a magaleta, ndi a anthu ndi a miyoyo ya anthu. Ndipo zokhumbitsa moyo wako zidakuchokera; ndipo zonse zolongosoka, ndi zokometsetsa zakutayikira, ndipo izi sudzazipezanso konse. Otsatsa izi, olemezedwa nao, adzaima patali chifukwa cha kuopa chizunzo chake, nadzalira, ndi kuchita chifundo; nadzanena, Tsoka, tsoka, mudzi waukulu wovala bafuta ndi chibakuwa, ndi mlangali, wodzikometsera ndi golide ndi mwala wa mtengo wake, ndi ngale! Pakuti m'ora limodzi chasanduka bwinja chuma chachikulu chotere. Ndipo watsigiro aliyense, ndi yense wakupita panyanja pakutipakuti, ndi amalinyero, ndi onse amene amachita kunyanja, anaima patali, nafuula poona utsi wa kutentha kwake, nanena, Mudzi uti ufanana ndi mudzi waukuluwo? Ndipo anathira fumbi pamitu pao, nafuula, ndi kulira, ndi kuchita maliro, nanena, Tsoka, tsoka, mudzi waukuluwo, umene analemerezedwa nao onse akukhala nazo zombo panyanja, chifukwa cha kulemera kwake, pakuti m'ora limodzi unasanduka bwinja. Kondwera pa iye, m'mwamba iwe, ndi oyera mtima, ndi atumwi, ndi aneneri inu; chifukwa Mulungu anauweruzira kuweruzidwa kwanu. Ndipo mngelo wolimba ananyamula mwala ngati mphero yaikulu, naiponya m'nyanja, nanena, Chotero Babiloni, mudzi waukulu, udzapasulidwa kolimba, ndipo sudzapezedwanso konse. Ndipo mau a anthu oimba zeze, ndi a oimba, ndi a oliza zitoliro, ndi a oomba malipenga sadzamvekanso konse mwa iwe; ndipo mmisiri aliyense wa machitidwe ali onse sadzapezedwanso konse mwa iwe; ndi mau a mphero sadzamvekanso konse mwa iwe; ndi kuunika kwa nyali sikudzaunikiranso konse mwa iwe; ndi mau a mkwati ndi a mkwatibwi sadzamvekanso konse mwa iwe; pakuti otsatsa malonda anu anali omveka a m'dziko; pakuti ndi nyanga yako mitundu yonse inasokeretsedwa. Ndipo momwemo munapezedwa mwazi wa aneneri ndi oyera mtima, ndi onse amene anaphedwa padziko. Zitatha izi ndinamva ngati mau akulu a khamu lalikulu m'Mwamba, lili kunena, Aleluya; chipulumutso, ndi ulemerero, ndi mphamvu, nza Mulungu wathu; pakuti maweruzo ake ali oona ndi olungama; ndipo anaweruza mkazi wachigololo wamkulu, amene anaipsa dziko ndi chigololo chake, ndipo anabwezera chilango mwazi wa akapolo ake pa dzanja lake la mkaziyo. Ndipo anatinso, Aleluya. Ndipo utsi wake ukwera kunthawi za nthawi. Ndipo anagwa pansi akuluwo makumi awiri mphambu anai ndi zamoyo zinai, ndipo zinalambira Mulungu wakukhala pa mpando wachifumu, nizinena, Amen; Aleluya. Ndipo mau anachokera kumpando wachifumu, ndi kunena, Lemekezani Mulungu wathu akapolo ake onse akumuopa Iye, ang'ono ndi akulu. Ndipo ndinamva ngati mau a khamu lalikulu, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati mau a mabingu olimba, nizinena, Aleluya; pakuti achita ufumu Ambuye Mulungu wathu, Wamphamvuyonse. Tikondwere, tisekerere, ndipo tipatse ulemerero kwa Iye; pakuti wadza ukwati wa Mwanawankhosa; ndipo mkazi wake wadzikonzera. Ndipo anampatsa iye avale bafuta wonyezimira woti mbu; pakuti bafuta ndiye zolungama za oyera mtima. Ndipo ananena ndi ine, Lemba, Odala iwo amene aitanidwa kuphwando la ukwati wa Mwanawankhosa. Ndipo ananena ndi ine, Iwo ndiwo mau oona a Mulungu. Ndipo ndinagwa pa mapazi ake kumlambira iye. Ndipo ananena ndi ine, Tapenya, usatero; ine ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako akukhala nao umboni wa Yesu; lambira Mulungu: pakuti umboni wa Yesu ndiwo Mzimu wa chinenero. Ndipo ndinaona mutatseguka m'Mwamba; ndipo taonani, kavalo woyera, ndi Iye wakumkwera wotchedwa Wokhulupirika ndi Woona; ndipo aweruza, nachita nkhondo molungama. Ndipo maso ake ali lawi la moto, ndi pamutu pake pali nduwira zachifumu zambiri; ndipo ali nalo dzina lolembedwa, wosalidziwa wina yense koma Iye yekha. Ndipo avala chovala chowazidwa mwazi; ndipo atchedwa dzina lake, Mau a Mulungu. Ndipo magulu a nkhondo okhala m'Mwamba anamtsata Iye, okwera pa akavalo oyera, ovala bafuta woyera woti mbu. Ndipo m'kamwa mwake mutuluka lupanga lakuthwa, kuti akanthe nalo mitundu ya anthu; ndipo Iye adzawalamulira ndi ndodo yachitsulo: ndipo aponda Iye moponderamo mphesa mwa vinyo waukali wa mkwiyo wa Mulungu Wamphamvuyonse. Ndipo ali nalo pa chovala chake ndi pa ntchafu yake dzina lolembedwa, MFUMU YA MAFUMU, NDI MBUYE WA AMBUYE. Ndipo ndinaona mngelo alikuima m'dzuwa; ndipo anafuula ndi mau akulu akunena ndi mbalame zonse zakuuluka pakati pa mlengalenga: Idzani kuno, sonkhanani kuphwando la Mulungu wamkulu, kuti mudzadye nyama ya mafumu, ndi nyama ya akapitao, ndi nyama ya anthu amphamvu, ndi nyama ya akavalo, ndi ya iwo akukwerapo, ndi nyama ya anthu onse, mfulu ndi akapolo, ndi ang'ono ndi akulu. Ndipo ndinaona chilombocho, ndi mafumu a dziko, ndi magulu a nkhondo ao, osonkhanidwa kuchita nkhondo pa Iye wakukwera pa kavalo, ndi gulu la nkhondo lake. Ndipo chinagwidwa chilombocho, ndi pamodzi nacho mneneri wonyenga amene adachita zizindikiro pamaso pake, zimene anasokeretsa nazo iwo amene adalandira lemba la chilombo, ndi iwo akulambira fano lake; iwo awiri anaponyedwa ali moyo m'nyanja yamoto yakutentha ndi sulufure: ndipo otsalawa anaphedwa ndi lupanga la Iye wakukwera pa kavalo, ndilo lotuluka m'kamwa mwake; ndipo mbalame zonse zinakhuta ndi nyama zao. Ndipo ndinaona mngelo anatsika Kumwamba, nakhala nacho chifungulo cha ku chiphompho chakuya, ndi unyolo waukulu m'dzanja lake. Ndipo anagwira chinjoka, njoka yakaleyo, ndiye mdierekezi ndi Satana, nammanga iye zaka chikwi, namponya ku chiphompho chakuya, natsekapo, nasindikizapo chizindikiro pamwamba pake, kuti asanyengenso amitundu kufikira kudzatha zaka chikwi; patsogolo pake ayenera kumasulidwa iye kanthawi. Ndipo ndinaona mipando yachifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa chiweruziro; ndipo ndinaona mizimu ya iwo amene adawadula khosi chifukwa cha umboni wa Yesu, ndi chifukwa cha mau a Mulungu, ndi iwo amene sanalambira chilombo, kapena fano lake, nisanalandira lembalo pamphumi ndi pa dzanja lao; ndipo anakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndi Khristu zaka chikwi. Otsala a akufa sanakhalanso ndi moyo kufikira kudzatha zaka chikwi. Ndiko kuuka kwa akufa koyamba. Wodala ndi woyera mtima ali iye amene achita nao pa kuuka koyamba; pa iwowa imfa yachiwiri ilibe ulamuliro; komatu adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu, nadzachita ufumu pamodzi ndi Iye zaka chikwizo. Ndipo pamene zidzatha zaka chikwi, adzamasulidwa Satana m'ndende yake; nadzatuluka kudzasokeretsa amitundu ali mungodya zinai za dziko, Gogi, ndi Magogi, kudzawasonkhanitsa achite nkhondo: chiwerengero chao cha iwo amene chikhala ngati mchenga wa kunyanja. Ndipo anakwera nafalikira m'dziko, nazinga tsasa la oyera mtima ndi mudzi wokondedwawo: ndipo unatsika moto wakumwamba nuwanyeketsa. Ndipo mdierekezi wakuwasokeretsa anaponyedwa m'nyanja ya moto ndi sulufure, kumeneko kulinso chilombocho ndi mneneri wonyengayo; ndipo adzazunzidwa usana ndi usiku kunthawi za nthawi. Ndipo ndinaona, mpando wachifumu waukulu woyera, ndi Iye wakukhalapo, amene dziko ndi m'mwamba zinathawa pamaso pake, ndipo sanapezedwa malo ao. Ndipo ndinaona akufa, akulu ndi ang'ono alinkuima kumpando wachifumu; ndipo mabuku anatsegulidwa; ndipo buku lina linatsegulidwa, ndilo la moyo; ndipo akufa anaweruzidwa mwa zolembedwa m'mabuku, monga mwa ntchito zao. Ndipo nyanja inapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi dziko la akufa zinapereka akufawo anali m'menemo; ndipo anaweruzidwa yense monga mwa ntchito zake. Ndipo imfa ndi dziko la akufa zinaponyedwa m'nyanja yamoto. Iyo ndiyo imfa yachiwiri, ndiyo nyanja yamoto. Ndipo ngati munthu sanapezedwa wolembedwa m'buku la moyo, anaponyedwa m'nyanja yamoto. Ndipo ndinaona m'mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano; pakuti m'mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidachoka, ndipo kulibenso nyanja. Ndipo ndinaona mzinda woyerawo, Yerusalemu watsopano, ulikutsika Kumwamba kwa Mulungu, wokonzeka ngati mkwatibwi wokometsedwera mwamuna wake. Ndipo ndinamva mau akulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pao; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita. Ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu anati, Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano. Ndipo ananena, Talemba; pakuti mau awa ali okhulupirika ndi oona. Ndipo anati kwa ine, Zatha. Ine ndine Alefa ndi Omega, Woyamba ndi Wotsiriza. Kwa iye wakumva ludzu ndidzampatsa amwe kukasupe wa madzi a moyo kwaulere. Iye wakupambana adzalandira izi; ndipo ndidzakhala Mulungu wake, ndi iye adzakhala mwana wanga. Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, cholandira chao chidzakhala m'nyanja yotentha ndi moto ndi sulufure; ndiyo imfa yachiwiri. Ndipo anadza mmodzi wa angelo asanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, zodzala ndi miliri yotsiriza isanu ndi iwiri; ndipo analankhula ndi ine, nanena, Idza kuno, ndidzakuonetsa mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa. Ndipo ananditenga mu Mzimu kunka kuphiri lalikulu ndi lalitali, nandionetsa mzinda wopatulikawo, Yerusalemu, wotsika m'Mwamba kuchokera kwa Mulungu, ndipo unakhala nao ulemerero wa Mulungu; kuunika kwake kunafanana ndi mwala wa mtengo wake woposa, ngati mwala wayaspi, wonyezimira, ngati krustalo; nukhala nalo linga lalikulu ndi lalitali, nukhala nazo zipata khumi ndi ziwiri, ndi pazipata angelo khumi ndi awiri, ndi maina olembedwapo, ndiwo maina a mafuko khumi ndi awiri a ana a Israele; kum'mawa zipata zitatu, ndi kumpoto zipata zitatu, ndi kumwera zipata zitatu, ndi kumadzulo zipata zitatu. Ndipo linga la mudzi linakhala nao maziko khumi ndi awiri, ndi pomwepo maina khumi ndi awiri a atumwi khumi ndi awiri a Mwanawankhosa. Ndipo iye wakulankhula ndi ine anali nao muyeso, bango lagolide, kuti akayese mzindawo, ndi zipata zake, ndi linga lake. Ndipo mzinda ukhala waphwamphwa; utali wake ulingana ndi kupingasa kwake: ndipo anayesa mzinda ndi bangolo, mastadiya zikwi khumi ndi ziwiri; utali wake, ndi kupingasa kwake, ndi kutalika kwake zilingana. Ndipo anayesa linga lake, mikono zana mphambu makumi anai kudza zinai, muyeso wa munthu, ndiye mngelo. Ndipo mirimo ya linga lake ndi yaspi; ndipo mzindawo ngwa golide woyengeka, wofanana ndi mandala oyera. Maziko a linga la mzinda anakometsedwa ndi miyala ya mtengo, ya mitundumitundu; maziko oyamba, ndi yaspi; achiwiri, ndi safiro; achitatu, ndi kalikedo; achinai, ndi smaragido; achisanu, ndi sardonu; achisanu ndi chimodzi, ndi sardiyo; achisanu ndi chiwiri, ndi krusolito; achisanu ndi chitatu, ndi berulo; achisanu ndi chinai, ndi topaziyo; akhumi, ndi krusoprazo; akhumi ndi achimodzi, ndi huakinto; akhumi ndi chiwiri, ndi ametusto. Ndipo zitseko khumi ndi ziwiri ndizo ngale khumi ndi ziwiri; chitseko chilichonse pa chokha cha ngale imodzi. Ndipo khwalala la mzinda nla golide woyengeka, ngati mandala openyekera. Ndipo sindinaona Kachisi momwemo; pakuti Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, ndi Mwanawankhosa ndiwo Kachisi wake. Ndipo pamzinda sipafunika dzuwa, kapena mwezi wakuuwalira; pakuti ulemerero wa Mulungu uunikira umenewu, ndipo nyali yake ndiye Mwanawankhosa. Ndipo amitundu adzayendayenda mwa kuunika kwake; ndi mafumu a dziko atenga ulemerero wao kulowa nao momwemo. Ndipo pazipata zake sipatsekedwa konse usana, (pakuti sikudzakhala usiku komweko); ndipo adzatenga ulemerero ndi ulemu wa amitundu nadzalowa nao momwemo; ndipo simudzalowa konse momwemo kanthu kalikonse kosapatulidwa kapena iye wakuchita chonyansa ndi bodza; koma iwo okha olembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa. Ndipo anandionetsa mtsinje wa madzi a moyo, wonyezimira ngati krustalo, otuluka kumpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa. Pakati pa khwalala lake, ndi tsidya ili la mtsinje, ndi tsidya lake lija panali mtengo wa moyo wakubala zipatso khumi ndi ziwiri, ndi kupatsa zipatso zake mwezi ndi mwezi; ndipo masamba a mtengo ndiwo akuchiritsa nao amitundu. Ndipo sipadzakhalanso temberero lililonse; ndipo mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa udzakhala momwemo; ndipo akapolo ake adzamtumikira Iye, nadzaona nkhope yake; ndipo dzina lake lidzakhala pamphumi pao. Ndipo sikudzakhalanso usiku; ndipo sasowa kuunika kwa nyali, ndi kuunika kwa dzuwa; chifukwa Ambuye Mulungu adzawaunikira; ndipo adzachita ufumu kunthawi za nthawi. Ndipo anati kwa ine, Mau awa ali okhulupirika ndi oona; ndipo Ambuye, Mulungu wa mizimu ya aneneri, anatuma mngelo wake kukaonetsera akapolo ake zimene ziyenera kuchitika msanga. Ndipo taonani, ndidza msanga. Wodala iye amene asunga mau a chinenero cha buku ili. Ndipo ine Yohane ndine wakumva ndi wakupenya izi. Ndipo pamene ndinamva ndi kupenya, ndinagwa pansi kulambira pa mapazi a mngelo wakundionetsa izo. Ndipo ananena kwa ine, Tapenya, usachite; ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako aneneri, ndi wa iwo akusunga mau a buku ili; lambira Mulungu. Ndipo ananena ndi ine, Usasindikiza chizindikiro mau a chinenero cha buku ili; pakuti nthawi yayandikira. Iye wakukhala wosalungama achitebe zosalungama; ndi munthu wonyansa akhalebe wonyansa; ndi iye wakukhala wolungama achitebe cholungama; ndi iye amene ali woyera akhalebe woyeretsedwa. Taonani, ndidza msanga; ndipo mphotho yanga ndili nayo yakupatsa yense monga mwa ntchito yake. Ine ndine Alefa ndi Omega, Woyamba ndi Wotsiriza, Chiyambi ndi Chitsiriziro. Odala iwo amene atsuka miinjiro yao, kuti akakhale nao ulamuliro pa mtengo wa moyo, ndi kuti akalowe m'mzinda pazipata. Kunja kuli agalu ndi anyanga, ndi achigololo, ndi ambanda, ndi opembedza mafano, ndi yense wakukonda bodza ndi kulichita. Ine Yesu ndatuma mngelo wanga kukuchitirani umboni za izi m'Mipingo. Ine ndine muzu ndi mbadwa ya Davide, nyenyezi yonyezimira ya nthanda. Ndipo Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani. Ndipo wakumva anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere. Ndichita umboni kwa munthu aliyense wakumva mau a chinenero cha buku ili, Munthu akaonjeza pa awa, adzamuonjezera Mulungu miliri yolembedwa m'bukumu: ndipo aliyense akachotsako pa mau a buku la chinenero ichi, Mulungu adzamchotsera gawo lake pa mtengo wa moyo, ndi m'mzinda woyerawo, ndi pa izi zilembedwa m'bukumu. Iye wakuchitira umboni izi, anena, Indetu; ndidza msanga. Amen; idzani, Ambuye Yesu. Chisomo cha Ambuye Yesu chikhale ndi oyera mtima onse. Amen.