Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi. Dziko lapansilo linali lopanda maonekedwe enieni ndiponso losakonzeka. Mdima unali utaphimba nyanja yaikulu ponseponse, ndipo Mzimu wa Mulungu unkayendayenda pamwamba pa madziwo. Tsono Mulungu adati, “Kuyere,” ndipo kudayeradi. Mulungu adaona kuti kuyerako kunali kwabwino. Pomwepo adalekanitsa kuyerako ndi mdima. Kuyerako adakutcha Usana, mdima uja adautcha Usiku. Ndipo kudali madzulo ndiponso m'maŵa, tsiku loyamba. Kenaka Mulungu adati, “Pakhale cholekanitsa madzi, kuti madziwo akhale pa malo aŵiri olekana,” ndipo zidachitikadi. Motero Mulungu adalenga cholekanitsa madzi chija, naŵagaŵa madziwo, ena pansi pa cholekanitsacho ena pamwamba pake. Cholekanitsacho adachitcha dzina loti Thambo. Ndipo kudali madzulo ndiponso m'maŵa, tsiku lachiŵiri. Mulungu adatinso, “Madzi apansiŵa akhale pa malo amodzi, kuti paoneke mtunda,” ndipo zidachitikadi. Mulungu adautcha mtundawo Dziko, madzi adaŵasonkhanitsa aja adaŵatcha Nyanja. Mulungu adaona kuti zinali zabwino. Tsono adati, “Panthaka pamere zomera zobala njere, ndiponso mitengo yobala zipatso zanjere malinga ndi mtundu wake,” ndipo zidachitikadi. Motero panthaka padamera zomera za mitundu yonse, zipatso zokhala ndi njere ndi mitengo yobeleka zipatso za njere, malingana ndi mitundu yao. Mulungu adaona kuti zinali zabwino. Ndipo kudali madzulo ndiponso m'maŵa, tsiku lachitatu. Pambuyo pake Mulungu adati, “Kuthambo kukhale miyuni kuti izilekanitsa usana ndi usiku, ndiponso kuti ikhale zizindikiro za nyengo, masiku ndi zaka. Miyuni imeneyi ikhale ku thambo ndi kumaunikira dziko lapansi,” ndipo zidachitikadi. Motero Mulungu adalenga miyuni iŵiri yaikulu: dzuŵa loŵala masana, ndi mwezi woŵala usiku. Adalenganso nyenyezi. Mulungu adaika miyuniyo ku thambo, kuti iziwunikira dziko lapansi, kuti iziŵala usana ndi usiku, kulekanitsa kuyera ndi mdima. Mulungu adaona kuti zinali zabwino. Ndipo kudali madzulo ndiponso m'maŵa, tsiku lachinai. Zitatero Mulungu adati, “M'nyanja mukhale zamoyo zambirimbiri, ndipo pakhale mbalame zouluka mu mlengalenga.” Motero Mulungu adalenga nsomba zazikulu zam'nyanja, pamodzi ndi zolengedwa zina zonse zokhala m'madzi, ndiponso mbalame ndi zouluka zina zamitundumitundu. Mulungu adaona kuti zonse zimene adalengazo zinali zabwino. Adazidalitsa ponena kuti, “Swanani ndipo mudzaze nyanja, mbalamenso ziswane pa dziko.” Tsono kudali madzulo ndiponso m'maŵa, tsiku lachisanu. Ndipo Mulungu adati, “Padziko pakhale mitundu yonse ya zamoyo potsata mitundu yake: zoŵeta, zokwaŵa, ndi nyama zakuthengo, potsata mitundu yake.” Ndipo zidachitikadi. Pomwepo Mulungu adalenga nyama zakuthengo potsata mitundu yake, ndi nyama zoŵeta potsata mitundu yake, ndiponso zokwaŵa zonse potsata mitundu yake. Mulungu adaona kuti zonse zimene adalengazo zinali zabwino. Zitatha izo Mulungu adati, “Tiyeni tipange munthu m'chifanizo chathu, adzakhale wonga Ifeyo. Adzalamulire nsomba zam'nyanja, mbalame zamumlengalenga, nyama zoŵeta, ndi zokwaŵa zonse za pa dziko lapansi.” Motero Mulungu adalenga munthu, m'chifanizo chake, adaŵalengadi m'chifanizo cha Mulungu. Adaŵalenga wina wamwamuna wina wamkazi. Adaŵadalitsa poŵauza kuti, “Mubereke ndi kuchulukana, mudzaze dziko lonse lapansi ndi kumalilamulira. Ndakupatsani ulamuliro pa nsomba, mbalame ndi nyama zonse zimene zikukhala pa dziko lapansi.” Ndipo Mulungu adati, “Ndikukupatsani zomera zonse za mtundu wokhala njere, ndi mitundu yonse ya zomera zobala zipatso zanjere, kuti muzidya. Koma nyama zonse zakuthengo, mbalame, ndi zokwaŵa zonse, ndazipatsa msipu kuti zizidya,” ndipo zidachitikadi momwemo. Mulungu adaona kuti zonse zimene adalengazo zinali zabwino kwambiri. Tsono kudali madzulo ndiponso m'maŵa, tsiku lachisanu ndi chimodzi. Motero dziko lonse lapansi, thambo ndi zonse zokhala m'menemo, zidatha kulengedwa. Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi Mulungu adamaliza ntchito imene ankachitayo, ndipo adapumula pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri. Mulungu adadalitsa tsiku lachisanu ndi chiŵirilo, naliyeretsa, chifukwa choti pa tsiku limenelo adapuma atatsiriza zonse zimene ankachita. Ndimo m'mene dziko lapansi ndi zonse zakuthambo zidalengedwera. Pamene Chauta ankalenga dziko lapansi ndi zonse zakuthambo, panalibe chomera chilichonse pa dziko lapansi, ndipo mbeu zinali zisanamere, chifukwa Chauta Mulungu anali asanagwetse mvula pa dziko lapansi. Ndipo panalibenso wina aliyense wolima pa nthaka. Koma madzi ankatuluka m'dziko lonse lapansi ndi kumathirira nthaka. Tsono Chauta adatenga dothi pa nthaka, ndipo adaumba munthu ndi dothilo. Adamuuzira mpweya wopatsa moyo m'mphuno zake, ndipo munthuyo adakhala wamoyo. Kenaka Chauta adatsekula munda mu Edeni chakuvuma, ndipo munthu adamuumbayo adamkhazika m'menemo. Chauta adameretsamo mitengo yokongola ya zipatso zokoma. Pakati pa mundawo panali mtengo wopatsa moyo, ndiponso mtengo wodziŵitsa zabwino ndi zoipa. Mtsinje wotuluka mu Edeni momwemo, unkayenda numathirira mundawo. Mtsinjewo udagaŵika panai, nusanduka mitsinje inai. Mtsinje woyamba ndi Pisoni, ndipo umayenda mozungulira dziko la Havila, kumene kumapezeka golide. (Golide wakumeneko ndi wabwino. Kumapezekanso bedeliyo ndi miyala ya mtengowapatali yotchedwa onikisi.) Mtsinje wachiŵiri ndi Gihoni, ndipo umayenda mozungulira dziko la Kusi. Mtsinje wachitatu ndi Tigrisi, umene umayenda kuvuma kwa Asiriya. Mtsinje wachinai ndi Yufurate. Tsono Chauta adamtenga munthuyo, namukhazika m'munda wa Edeni uja kuti azilima ndi kumausamala. Ndipo Chauta adamlamula munthuyo kuti, “Uzidya zipatso za mtengo uliwonse wam'mundawu, kupatula mtengo wokhawo umene umadziŵitsa zabwino ndi zoipa. Zipatso za mtengo umenewo usadye. Ukadzadya, ndithu udzafa!” Pambuyo pake Chauta adati, “Sibwino kuti munthuyu akhale yekha. Ndipanga mnzake woti azimthandiza.” Chauta adatenga dothi naumba nyama zonse ndi mbalame zonse, nabwera nazo kwa Adamu kuti azitche maina. Mwakuti maina amene Adamu adazitcha, maina ake ndi omwewo. Adamu adazitcha maina nyama zonse, mbalame ndi zamoyo zonse zakuthengo. Komabe panalibe mnzake woti azimthandiza. Tsono Chauta adagonetsa Adamu tulo tofanato, ndipo ali m'tulo choncho, Mulungu adamchotsako nthiti, natsekapo ndi mnofu pamalopo. Chauta Mulungu adapanga mkazi ndi nthiti imene adaichotsa kwa Adamu uja, ndipo mkaziyo Mulungu adabwera naye kwa iye. Adamu adati, “Uyutu ndiye ndi fupa lochokera ku mafupa anga, mnofu wochokera ku mnofu wanga. Adzatchedwa Mkazi, chifukwa watengedwa kwa Mwamuna.” Nchifukwa chake mwamuna amasiya atate ndi amai, ndipo amaphatikana ndi mkazi wake, choncho aŵiriwo amakhala thupi limodzi. Mwamunayo ndi mkazi wake uja, onse anali maliseche, komabe sankachita manyazi. Njoka inali yochenjera kupambana zamoyo zonse zimene Chauta adazilenga. Njokayo idafunsa mkazi uja kuti, “Kodi nzoona kuti Mulungu adakuletsani kuti musadye zipatso za mtengo uliwonse m'munda muno?” Mkazi uja adayankha kuti, “Tingathe kudya zipatso za mtengo uliwonse m'munda muno, kupatula wokhawo umene uli pakati pake. Mulungu adanena kuti tisadye zipatso za mtengo umenewo, ngakhale kuzikhudza, chifukwa choti tikadzangotero, tidzafa.” Koma njokayo idayankha mkaziyo kuti, “Iyai, kufa simudzafa konse. Mulungu amadziŵa kuti inu mukadzadya zipatso zimenezi, maso anu adzatsekuka, ndipo mudzakhala monga momwe aliri Mulunguyo. Mudzadziŵa zabwino ndi zoipa.” Tsono mkaziyo adaona kuti mtengowo ndi wokongola, ndiponso kuti zipatso zake zingakhale zokoma kudya. Pompo adayamba kukhumbira kuti adyeko zipatsozo, adzakhale wanzeru. Motero adathyolako zipatso zina za mtengowo, naadya. Tsono zina adapatsako mwamuna wake, ndipo iyenso adadya. Atangodya choncho, adazindikira kuti ali maliseche. Choncho adasoka masamba a mkuyu navala. Madzulo dzuŵa litapepa, aŵiriwo adamva mtswatswa, Chauta akuyenda m'mundamo, ndipo iwo adabisala m'katikati mwa mitengo, kuti Iye angaŵaone. Koma Chauta adamuitana Adamu uja kuti, “Kodi uli kuti?” Adamu adayankha kuti, “Ndinakumvani m'mundamu ndipo ndinaopa, ndiye ndinabisala ntaona kuti ndili maliseche.” Mulungu adamufunsa kuti, “Kodi adakuuza ndani kuti uli maliseche? Kapena wadyatu zipatso za mtengo uja ndidakuuza kuti usadyewu eti?” Pamenepo Adamu adayankha kuti, “Mkazi mudandipatsayu ndiye amene anandipatsa zipatsozo kuti ndidye, ndipo ndadyadi.” Apo Chauta adafunsa mkazi kuti, “Kodi iwe, zimene wachitazi wachitiranji?” Mkazi uja adayankha kuti, “Njoka ndiyo imene inandinyenga kuti ndidye.” Pamenepo Chauta adauza njokayo kuti, “Chifukwa chakuti wachita zimenezi, ndiwe wotembereredwa pakati pa nyama zonse za pansi pano, zoŵeta ndi zakuthengo zomwe. Kuyambira tsopano mpaka muyaya udzakwaŵa ndi kumimba kwako, ndipo chakudya chako chidzakhala fumbi. Ndidzaika chidani pakati pa iwe ndi mkazi, padzakhala chidani pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake. Idzaphwanya mutu wako, ndipo iwe udzaluma chidendene chake.” Pambuyo pake Mulungu adauza mkaziyo kuti, “Ndidzaonjeza zovuta zako pamene udzakhala ndi pathupi, udzamva zoŵaŵa pa nthaŵi yako ya kubala mwana. Udzakhumba mwamuna wako, ndipo mwamuna wakoyo adzakulamulira iwe.” Kenaka Mulungu adauza Adamu kuti, “Iwe unamvera mkazi wako, wadya zipatso zija zimene ndidaakuuza kuti usadye. Nthaka idzatembereredwa chifukwa cha zimene wachitazi. Udzayenera kugwira ntchito yathukuta nthaŵi ya moyo wako wonse, kuti upeze chakudya chokwanira. M'nthakamo mudzamera zitsamba za minga ndi za nthula, ndipo iwe udzadya zomera zakuthengo. Udzayenera kukhetsa thukuta kuti upeze chakudya, mpaka udzabwerera kunthaka komwe udachokera. Udachokera ku dothi, udzabwereranso kudothi komweko.” Adamu adatcha mkazi wake Heva, chifukwa choti iyeyu anali mai wa anthu onse. Ndipo Chauta adasokera Adamu ndi mkazi wake zovala zachikopa naŵaveka onse aŵiriwo. Chauta adati, “Tsopano munthuyu wakhala monga tiliri ife, popeza kuti akudziŵa zabwino ndi zoipa. Asaloledwe kudya zipatso za mtengo wopatsa moyowo ndi kukhala moyo mpaka muyaya.” Motero Chauta adamtulutsamo m'munda mwa Edeni muja, kuti azilima m'nthaka momwe adachokera. Atampirikitsira kunja Adamuyo, Mulungu adaika akerubi kuvuma kwa munda wa Edeni. Adaikanso lupanga lamoto limene linkazungulira mbali zonse, kutchinjiriza mtengo wopatsa moyo uja, kuti wina asaufike pafupi. Adamu adakhala ndi mkazi wake Heva ndipo mkaziyo adatenga pathupi. Tsono adabala mwana wamwamuna, ndipo adati, “Ndalandira mwana wamwamuna mwa chithandizo cha Chauta.” Motero mwanayo adamutcha Kaini. Pambuyo pake adabalanso Abele, mng'ono wa Kaini. Abele anali woŵeta nkhosa, koma Kaini anali mlimi. Patapita nthaŵi, Kaini adatenga zipatso zina zakumunda, nazipereka kwa Chauta. Abele nayenso adatenga ana oyamba kubadwa a nkhosa zake, naŵapereka ngati nsembe, pamodzi ndi mafuta ake omwe. Tsono Chauta adakondwera ndi Abele, nalandira nsembe yake. Koma Kaini Chauta sadakondwere naye ndipo sadalandire chopereka chake. Chifukwa cha zimenezi, Kainiyo adakwiya kwambiri, kotero kuti nkhope yake inali yakugwa ndi yamasinya. Apo Chauta adafunsa Kainiyo kuti, “Kodi wakwiyiranji chotere? Chifukwa chiyani nkhope yako yagwa? Ukadachita zabwino, ndikadakondwera nawe. Koma chifukwa choti wachita zoipa, tchimo lakukhalirira pa khomo ngati chilombo cholusa. Likulakalaka kuti likugwire, koma iweyo uligonjetse tchimolo.” Tsiku lina Kaini adauza mng'ono wake Abele kuti, “Tiye tikayende.” Atangopita kwa okha, Kaini adaukira mng'ono wakeyo namupha. Tsono Chauta adafunsa Kainiyo kuti, “Kodi mng'ono wako Abele ali kuti?” Iye adayankha kuti, “Sindikudziŵa. Kodi ndi ntchito yanga kusamala mng'ono wangayo?” Chauta adamufunsanso kuti, “Kodi wachita chiyani? Magazi a mng'ono wako akulira kwa Ine kuchokera m'nthaka. Tsopano watembereredwa, sudzailimanso nthaka yomwe yamwa magazi a mng'ono wako, amene waŵakhetsa ndi manja ako. Ukamalima mbeu, nthakayo sidzakubalira, ndipo udzakhala womangoyendayenda, wosoŵa pokhala penipeni pa dziko lapansi.” Kaini adauza Chauta kuti, “Chilango chimenechi nchopitirira mphamvu zanga. Tsopano mwandipirikitsa pa dziko ndi pamaso panu. Ndidzakhala wothaŵathaŵa pa dziko lapansi, ndipo aliyense wondipeza adzandipha.” Koma Chauta adamuyankha kuti, “Iyai, aliyense wopha iwe Kaini adzalangidwa, ndipo Ineyo ndidzamulipsira kasanunkaŵiri.” Motero Chauta adaika chizindikiro pa Kaini kuchenjeza aliyense kuti asamuphe Kainiyo. Tsono Kaini adachoka pamaso pa Chauta nakakhala m'dziko lotchedwa Nodi, kuvuma kwa Edeni. Kaini adakhala ndi mkazi wake, mkaziyo adatenga pathupi, nabala mwana dzina lake Enoki. Tsono Kaini adamanga mzinda, nautcha dzina la mwana wake Enoki. Enoki adabereka mwana namutcha Iradi. Iradi adabereka Mehuyaele. Mahuyaele adabereka Metusaele amene adabereka Lameki. Lameki adakwatira akazi aŵiri. Dzina la mkazi wake woyamba linali Ada, la mkazi wachiŵiri linali Zila. Ada adabala Yabala, ndipo iyeyu ndiye kholo la onse oŵeta zoŵeta ndi okhala m'mahema. Mbale wake anali Yubale, ndipo ndiye kholo la onse okhoza kuimba zeze ndi toliro. Zila adabala Tubala-Kaini. Iyeyu ndiye kholo la onse ogwira ntchito yosula mkuŵa ndi zitsulo. Mlongo wa Tubala-Kainiyo anali Naama. Tsono Lameki adauza akazi akewo kuti, “Iwe Ada ndi iwe Zila, mverani mau anga. Tcherani khutu mumve, inu akazi anga. Ine ndapha munthu chifukwa anandipweteka. Ndamuphadi mnyamatayo amene anandimenya. Ngati wopha Kaini amlipsira kasanunkaŵiri, ndiye kuti wopha ine Lameki adzamlipsira kokwanira 77.” Adamu adakhalanso ndi Heva mkazi wake, ndipo adatenga pathupi nabala mwana. Tsono Hevayo adati, “Mulungu wandipatsa mwana woloŵa m'malo mwa Abele uja amene adaphedwa ndi Kaini.” Mwanayo adamutcha Seti. Seti adabereka mwana namutcha Enosi. Nthaŵi imeneyo anthu adayamba kutama dzina la Chauta mopemba. Mndandanda wa mibadwo yochokera mwa Adamu udayenda motere: (Mulungu polenga Adamu, adampanga muchifaniziro chake. Adalenga mwamuna ndi mkazi, ndipo adaŵadalitsa, naŵatchula dzina loti Anthu.) Adamu ali wa zaka 130 adabereka mwana wofanafana ndi iye, namutcha Seti. Pambuyo pake Adamu adakhala ndi moyo zaka zinanso 800. Adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. Adamwalira ali wa zaka 930. Seti ali wa zaka 105, adabereka mwana dzina lake Enosi, ndipo adakhalanso ndi moyo zaka zina 807. Adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. Adamwalira ali wa zaka 912. Enosi ali wa zaka 90, adabereka mwana dzina lake Kenani, ndipo adakhalanso ndi moyo zaka zina 815. Adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. Adamwalira ali wa zaka 905. Kenani ali wa zaka 70, adabereka mwana dzina lake Mahalalele, ndipo adakhalanso ndi moyo zaka zina 840. Adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. Adamwalira ali wa zaka 910. Mahalalele ali wa zaka 65 adabereka Yaredi, ndipo adakhalanso ndi moyo zaka zina 830. Adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. Adamwalira ali wa zaka 895. Yaredi ali wa zaka 162, adabereka mwana dzina lake Enoki, ndipo adakhalanso ndi moyo zaka zina 800. Adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. Adamwalira ali wa zaka 962. Enoki ali wa zaka 65, adabereka mwana dzina lake Metusela. Enoki adakhala ndi moyo zaka zina 300, akuyanjana ndi Mulungu. Adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. Adamwalira ali wa zaka 365. Iyeyu adayanjana ndi Mulungu moyo wake wonse. Ndipo sadaonekenso, chifukwa choti Mulungu adamtenga. Metusela ali wa zaka 187, adabereka mwana dzina lake Lameki, ndipo adakhalanso ndi moyo zaka zina 782. Adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. Adamwalira ali wa zaka 969. Lameki ali wa zaka 182, adabereka mwana, ndipo adati, “Mwana ameneyu adzatipumuza ku ntchito zathu zolemetsazi zolima nthaka imene Chauta adaitemberera.” Ndipo mwanayo adamutcha dzina lake Nowa. Lameki adakhalanso ndi moyo zaka zina 595. Adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. Adamwalira ali wa zaka 777. Nowa ali wa zaka zopitirira 500, adabereka ana aamuna atatu: Semu, Hamu ndi Yafeti. Nthaŵi imeneyo anthu anali atayamba kuchuluka pa dziko lonse lapansi, ndipo adabereka ana aakazi. Ana aamuna a Mulungu adaona kuti ana aakazi a anthu anali okongola, nayamba kukwatira amene ankaŵakonda. Tsono Chauta adati, “Sindidzalola anthu kukhala ndi moyo mpaka muyaya, popeza kuti munthu ndi thupi limene limafa. Kuyambira tsopano adzangokhala zaka 120.” Pa masiku amenewo, ngakhale pambuyo pakenso, panali anthu amphamvu ataliatali pa dziko lapansi. Anthu ameneŵa ndi amene ankabadwa mwa akazi omwe adaakwatiwa ndi ana a Mulungu aja. Iwoŵa anali ngwazi zomveka ndiponso anthu otchuka pa masiku akalewo. Pamene Chauta adaona kuti anthu a pa dziko lapansi aipa koopsa, ndiponso kuti mitima yao inali yodzaza ndi maganizo oipa, adamva chisoni kuti adalenga anthu ndi kuŵakhazika pa dziko lapansi, ndipo adavutika mu mtima. Tsono adati, “Anthu onse amene ndaŵalenga, ndidzaŵaononga kotheratu. Ndidzaononganso nyama zonse ndi zokwaŵa zomwe pamodzi ndi mbalame, chifukwa ndikumva chisoni kuti ndidalenga zimenezi.” Koma Nowa yekha anali wangwiro pamaso pa Chauta. Nayi mbiri ya Nowa. Nowa anali munthu wochita zokondweretsa Mulungu, wopanda cholakwa, ndipo pa nthaŵi imeneyo adaali yekhayo amene anali wabwino pamaso pa Mulungu. Anali ndi ana aamuna atatu: Semu, Hamu ndi Yafeti. Koma anthu ena onse anali oipa pamaso pa Mulungu, ndipo kuipa kwao kudawanda ponseponse. Mulungu atayang'ana dziko lapansi, adaona kuti ndi lonyansa, chifukwa anthu onse anali oipa kwambiri. Choncho Mulungu adauza Nowa kuti, “Ndatsimikiza mu mtima kuti ndiwononge anthu onse. Ndidzaŵaononga kotheratu chifukwa dziko lonse lapansi ladzaza ndi ntchito zao zoipa. Udzipangire chombo ndipo uchipange ndi matabwa a mtengo wa mnjale. Upange zipinda m'menemo, ndipo uchimate phula kunja kwake ndi m'kati momwe. M'litali mwake mwa chombocho mukhale mamita 140. M'mimba mwake mukhale mamita 23, ndipo msinkhu wake ukhale wa mamita 13 ndi theka. Upange denga la chombocho, ndipo usiye mpata wa masentimita 50 pakati pa dengalo ndi mbali zake. Uchimange mosanjikiza, chikhale cha nyumba zitatu, ndipo m'mbali mwake mukhale chitseko. Ndidzagwetsa mvula yachigumula pa dziko lapansi, kuti iwononge zamoyo zonse. Zonse zapadziko zidzafa, koma iweyo ndidzachita nawe chipangano. Udzaloŵe m'chombomo iwe pamodzi ndi mkazi wako, ndi ana ako pamodzi ndi akazi ao. Ndipo udzatengenso nyama za mtundu uliwonse, yaimuna ndi yaikazi, kuti zisungidwe ndi moyo. Mbalame za mtundu uliwonse ndi nyama zazikulu ndi zokwaŵa zomwe, zidzaloŵe m'chombo kuti zisungidwe ndi moyo. Udzatengenso zakudya za mtundu uliwonse kuti inu ndi nyamazo muzidzadya.” Motero Nowa adachitadi zonse zimene Mulungu adamlamula. Chauta adauza Nowa kuti, “Loŵa m'chombo iwe pamodzi ndi banja lako. Iwe wekha ndakupeza kuti ndiwe wochita zondikondweretsa mu mbadwo uno. Tsono tenga magulu asanu ndi aŵiri a nyama, ziŵiriziŵiri, yaimuna ndi yaikazi, zimene amaperekera nsembe, ndipo utengenso nyama ziŵiriziŵiri, yaimuna ndi yaikazi, zosaperekera nsembe. Utengekonso mbalame ziŵiriziŵiri za mtundu uliwonse, magulu asanu ndi aŵiri. Uchite zimenezi pofuna kuti nyama ndi mbalame za mitundu yonse zisungidwe ndi moyo, ndipo kuti zidzaswanenso pa dziko lapansi. Pakangopita masiku asanu ndi aŵiri, ndidzagwetsa mvula pa dziko lapansi masiku makumi anai, usana ndi usiku, kuti zife zamoyo zonse zimene ndidazipanga.” Ndipo Nowa adachita zonse zimene Mulungu adamlamula. Nowa anali wa zaka 600 pamene chigumulacho chidafika pa dziko lapansi. Iyeyo ndi mkazi wake ndi ana ake aamuna ndi akazi ao adaloŵa m'chombo, kuthaŵa chigumulacho. Nyama zazimuna ndi zazikazi zimene anthu amaperekera nsembe, mbalame pamodzi ndi nyama zokwaŵa zomwe, Nowa adaloŵa nazo m'chombo, monga Mulungu adaalamulira. Patangopita masiku asanu ndi aŵiri, chigumula chidafika pa dziko lonse lapansi. Pa 17, mwezi wachiŵiri, Nowa ali wa zaka 600, akasupe onse a madzi ambiri okhala pansi pa dziko adatumphuka, ndipo kuthambo kudatsekukanso, kuti madzi akhuthuke. Choncho mvula idagwa pa dziko lapansi masiku makumi anai, usana ndi usiku. Pa tsiku lomwelo, Nowa ndi mkazi wake, pamodzi ndi ana ake aamuna, Semu, Hamu ndi Yafeti, ndi akazi ao, adaloŵa m'chombomo. Iwowo adaloŵa m'chombo pamodzi ndi mtundu uliwonse wa nyama zakuthengo, zoŵeta, nyama zokwaŵa ndi mbalame za mtundu uliwonse. Nowa adaloŵa m'chombomo pamodzi ndi zamoyo zonse zazimuna ndi zazikazi, monga Mulungu adaalamulira. Pomwepo Chauta adatseka pa khomo. Chigumula chidagundika masiku makumi anai pa dziko lapansi. Madzi adayamba kukwera pa dziko lapansi, ndipo chombo chidayamba kuyandama. Madziwo adanka nakwererakwerera, ndipo chombocho chidayandama pa madzi. Kukwera kwa madzi kudapitirira ndithu mpaka kumiza ndi mapiri aatali omwe. Tsono adakwererakwerera ndithu mpaka kubzola nsonga za mapiriwo mamita asanu ndi aŵiri. Zamoyo zonse zokhala pa dziko lapansi zidafa, monga mbalame, zoŵeta, nyama zakuthengo, mtindiri wa tizilombo tosiyanasiyana, ndi anthu onse. Zamoyo zonse za pa dziko lapansi zidafa. Chauta adaononga zamoyo zonse za pa dziko: anthu, nyama, zokwaŵa ndi mbalame. Nowa yekha adapulumuka pamodzi ndi onse amene anali naye m'chombomo. Madziwo adakhala osaphwa konse pa dziko lapansi masiku 150. Tsono Mulungu adakumbukira Nowa pamodzi ndi nyama zonse zakuthengo ndi zoŵeta zimene zinali naye m'chombomo. Adalamula mphepo kuti iwombe pa dziko lapansi, pomwepo madzi adayamba kutsika. Akasupe a madzi ambiri okhala pansi pa dziko pamodzi ndi zipata zakuthambo, adazitseka. Mvula adailetsa, ndipo madzi adayamba kutsika pang'onopang'ono. Masiku 150 atapita, madziwo anali atatsika ndithu, ndipo pa tsiku la 17, mwezi wachisanu ndi chiŵiri, chombocho chidakaima pamwamba pa phiri la Ararati. Madziwo adanka natsikabe, ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wakhumi, nsonga za mapiri zidayamba kuwoneka. Patapita masiku makumi anai, Nowa adatsekula zenera, natulutsa khwangwala. Khwangwalayo ankangouluka mu mlengalenga kudikira kuti madzi aphwe pa dziko lapansi. Tsono Nowa adatulutsa nkhunda kuti ikaone ngati madzi aphwa. Koma popeza kuti madzi anali akadalipobe pa dziko lonse, nkhundayo idabwerera, chifukwa idaasoŵa potera. Nowa adatambalitsa dzanja kunja, nailoŵetsanso m'chombo muja. Atadikira masiku asanu ndi aŵiri ena, adaitulutsanso nkhunda ija m'chombo. Madzulo idabwerako, ndipo Nowa adaona kuti kukamwa kwake kuli tsamba laliŵisi la mtengo wa olivi. Apo Nowa adadziŵa kuti madzi ayamba kuphwa. Pambuyo pake Nowa atadikiranso masiku ena asanu ndi aŵiri, adaitulutsanso nkhunda ija, koma nkhundayo sidabwererenso. Nowa ali wa zaka 601, pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, madzi adaphweratu pa dziko lapansi. Nowa adatsekula zenera la chombo chija nayang'ana kunja, nkuwona kuti pansi pauma, Pa tsiku la 27 mwezi wachiŵiri, dziko lonse lapansi linali litauma kotheratu. Mulungu adauza Nowa kuti, “Iwe ndi mkazi wako, ana ako pamodzi ndi akazi ao, tulukani m'chombomo. Tulutsa zamoyo zonse zili ndi iwezo, mbalame, nyama ndi zokwaŵa, kuti ziswane ndi kubalalika pa dziko lonse lapansi.” Motero Nowa adatuluka m'chombo, iye ndi mkazi wake ndiponso ana ake ndi akazi ao. Nyama zonse, zokwaŵa zonse, mbalame zonse, ndi zina zonse zoyenda pansi pano zidatuluka m'chombomo m'magulumagulu potsata mitundu yake. Pamenepo Nowa adamanga guwa kumangira Chauta. Adatengako mtundu uliwonse wa nyama ndi mbalame zimene anthu amaperekera nsembe, ndipo adazipha, napereka nsembe zopsereza paguwapo. Chauta atamva fungo lokomalo, adati, “Sindidzatembereranso dziko chifukwa cha zochita za anthu, chifukwa ndikudziŵa maganizo a munthu kuti ndi oipa kuyambira ali mwana. Sindidzaononganso zamoyo zonse monga ndachitiramu. “Nthaŵi zonse m'mene dziko lapansi lidzakhalire, padzakhala nyengo yobzala ndi nyengo yokolola. Padzakhala nyengo yachisanu ndi nyengo yotentha, nyengo yachilimwe ndi nyengo yadzinja, ndipo usana ndi usiku zidzakhalapo kosalekeza.” Mulungu adadalitsa Nowa ndi ana ake omwe, nati “Mubale ana ambiri ndi kuchulukana, kuti mudzaze dziko lonse lapansi. Zamoyo zonse za pa dziko lapansi pamodzi ndi mbalame zomwe, nyama zokwaŵa ndi zonse zam'nyanja zidzakuwopani. Zonsezi ndaziika kuti muzilamule. Tsopano mungathe kudya nyama zonse, monga ndidakulolani kudya ndiwo zamasamba. Ndakupatsani zonsezi kuti zikhale chakudya chanu. Koma pali chinthu chimodzi chokha chimene simuyenera kudya, ndicho nyama imene ikali ndi magazi. Ndaletsa poti magaziwo ndiwo moyo wake. Aliyense wopha munthu, adzaphedwa. Nyama iliyonse yopha munthu, idzaphedwa. Munthu aliyense wopha mnzake, iyenso aphedwe. “Aliyense wopha munthu, nayenso adzaphedwa, pakuti munthu adalengedwa muchifaniziro cha Mulungu. Tsopano mubalane, kuti zidzukulu zanu zidzachulukane ndi kudzabalalika pa dziko lonse lapansi.” Mulungu adauza Nowa ndi ana ake kuti, “Tsopano ndikuchita nanu chipangano, pamodzi ndi zidzukulu zanu, ndi zamoyo zonse, mbalame, zoŵeta, nyama zakuthengo, ndi zina zonse zimene zidatuluka nanu m'chombo. Chipanganocho ndi ichi: ‘Ndikulonjeza kuti sindidzaononganso zamoyo zonse ndi chigumula. Ndithu chigumula sichidzaononganso dziko lapansi.’ ” Ndipo Mulungu adati, “Nachi chizindikiro cha chipangano chamuyaya chimene ndikuchiika pakati pa Ine ndi inu ndi cholengedwa chilichonse chimene chili ndi inu. Ndikuika utawaleza m'mitambo, ndipo udzakhala chizindikiro cha chipangano pakati pa Ine ndi dziko lapansi. Nthaŵi zonse pakakhala mitambo mu mlengalenga, ndipo pakaoneka utawaleza m'mitambomo, ndizidzakumbukira lonjezo langa limene ndidachita ndi inu ndi nyama zonse, kuti chigumula chisadzaonongenso zamoyo zonse. Utawaleza ukamadzaoneka m'mitambo, Ine ndidzaupenya, ndipo ndizidzakumbukira chipangano chamuyaya cha pakati pa Ine ndi zamoyo zonse zokhala pa dziko lapansi. Chimenechi ndi chizindikiro cha chipangano chimene ndachita ndi zamoyo zonse za pa dziko lapansi.” Ana a Nowa omwe adatuluka m'chombo muja anali Semu, Hamu ndi Yafeti. Hamu ndiye anali bambo wa Kanani. Ana a Nowa atatu ameneŵa ndiwo makolo a anthu a pa dziko lonse lapansi. Nowa anali mlimi ndipo anali woyamba kulima munda wamphesa. Tsiku lina atangomwa vinyo, adaledzera, ndipo adavula zovala zake zonse, nakagona ali maliseche m'hema mwake. Hamu, bambo wake wa Kanani, ataona kuti Nowa bambo wake ali maliseche, adapita nakauza abale ake aŵiri aja. Koma Semu ndi Yafeti adatenga chofunda nachiika kumbuyo kwao, atachinyamula pa mapewa. Tsono adayenda chafutambuyo nafunditsa bambo wao. Sadapenyeko kumene kunali bambo wao uja ndipo sadaone maliseche ake. Nowa atadzuka, adamva zonse zimene mwana wake wamng'onoyo adaachita, ndipo adati, “Atembereredwe Kanani! Adzakhala kapolo weniweni wa abale ake.” Popitiriza mau adati, “Atamandike Chauta, Mulungu wa Semu, Kanani adzakhale kapolo wa Semuyo. Mulungu amkuze Yafeti. Zidzukulu zake zidzagaŵane madalitso ndi zidzukulu za Semu. Kanani adzakhale kapolo wa Yafetiyo.” Chitatha chigumulacho, Nowa adakhala ndi moyo zaka zina 350. Adamwalira ali wa zaka 950. Nayi mibadwo ya ana a Nowa: Semu, Hamu ndi Yafeti. Atatu ameneŵa adabereka ana ao chitatha chigumula chija. Ana a Yafeti anali Gomeri, Magogi, Madai, Yavani, Tubala, Meseki ndi Tirasi. Ana a Gomeri anali Asikenazi, Rifati ndi Togarima. Ana a Yavani anali Elisa, Tarisisi, Kitimu ndi Dodanimu. Iwoŵa ndiwo anali makolo a onse amene ankakhala m'mbali mwa nyanja, ndi pa zilumba zam'nyanja. Ameneŵa ndiwo ana a Yafeti. Mafuko ao anali osiyanasiyana, ndipo ankakhala m'maiko osiyanasiyana. Fuko lililonse linkalankhula chilankhulo chakechake. Ana a Hamu anali Kusi, Ejipito, Libia ndi Kanani. Ana a Kusi anali Seba, Havila, Sabita, Raama ndi Sabiteka. Ana a Raama anali Sheba ndi Dedani. Kusi adabereka Nimirodi. Nimirodi anali wankhondo woyamba wanyonga pa dziko lapansi. Iyeyu analinso mlenje wamkulu pamaso pa Chauta. Nchifukwa chake anthu ali ndi chisudzo chakuti, “Ndiwe mlenje wamkulu pamaso pa Chauta, ngati Nimirodi.” Ankalamulira ku Babiloni, ku Ereki, ndi ku Akadi. Maufumu onseŵa anali m'dziko la Sinara. Iyeyu adachoka ku Sinara nakakhala ku Asiriya, ndipo adakamanga mizinda ya Ninive, Rehobotiiri, Kala, ndi mzinda wa Reseni umene uli pakati pa Ninive ndi mzinda waukulu uja wa Kala. Ejipito ndi amene anali kholo la anthu a ku Ludi, Anamu, Lehabu, Nafutu, Patirusi, Kasilu ndi Kafitori, makolo a Afilisti. Kanani adabereka mwana wake wachisamba dzina lake Sidoni, ndipo adaberekanso Heti. Ameneŵa adabereka Ayebusi, Aamori, Agirigasi. Ahivi, Aariki, Asini, Aaravadi, Azemari ndi Ahamati. Pambuyo pake mafuko a Akananiwo adabalalika ponseponse, mpaka ku malire a Kanani. Malirewo adayambira ku Sidoni namaloŵa ku Gerari mpaka ku Gaza ndi kumaloŵanso ku Sodomu, Gomora, Adima ndi Zeboimu mpaka ku Lasa. Ameneŵa ndiwo ana a Hamu ndipo ankakhala m'mafuko osiyanasiyana, ndi m'maiko osiyanasiyana. Fuko lililonse linkalankhula chilankhulo chakechake. Semu ndiye kholo la ana onse a Eberi, ndiponso ndiye mkulu wake wa Yafeti. Iyeyu anali ndi ana. Ana a Semu anali Elamu, Asuri, Aripakisadi, Ludi ndi Aramu. Ana a Aramu anali Uzi, Hulu, Getere ndi Masi. Aripakisadi adabereka Sela, ndipo Sela adabereka Eberi. Eberi anali ndi ana aŵiri. Wina anali Pelegi, chifukwa pa nthaŵi ya moyo wake, anthu onse a pa dziko lapansi anali ogaŵikana. Dzina la mbale wake linali Yokotani. Yokotani adabereka Alimodadi, Selefi, Hazara-Maveti, Yera, Hadoramu, Uzali, Dikila, Obala, Abimaele, Sheba, Ofiri, Havila ndi Yobabu. Onseŵa anali ana a Yokotani. Dziko limene ankakhalamo lidayambira ku Mesa kumaloŵa ku Sefari ku mapiri chakuvuma. Ameneŵa ndiwo zidzukulu za Semu. Mafuko ao anali osiyanasiyana, ndipo ankakhalanso m'maiko osiyanasiyana. Fuko lililonse linkalankhula chilankhulo chakechake. Onseŵa ndiwo mafuko a zidzukulu za Nowa potsata mibadwo yao ndi mitundu yao. Mitundu yonse ya pa dziko lapansi idatuluka mwa mafuko a Nowa ameneŵa, chitatha chigumula chija. Poyambayamba anthu onse a pa dziko lapansi ankalankhula chilankhulo chimodzi, ndipo mau amene ankalankhulawo anali amodzi. Atasamukira chakuvuma, adakafika ku chigwa ku dziko la Sinara kumene adakhazikika. Tsono adayamba kuuzana kuti, “Tiyeni tiwumbe njerwa ndi kuzitentha.” Motero m'malo mwa miyala adatenga njerwa, namangira phula m'malo mwa matope. Ndipo adati, “Tsopano tiyeni timange mzinda wathu, ndipo nsanja yake italike mpaka kukafika kumwamba. Tikatero tidzatchuka ndithu, ndipo sitidzamwazikanso pa dziko lapansi.” Tsono Chauta adatsika kudzaona mzindawo, pamodzi ndi nsanja imene anthu ankamanga. Ndipo adati, “Tsopano anthu onseŵa ndi amodzi, ndipo akulankhula chilankhulo chimodzi. Zinthu akuchitazi ndi chiyambi chabe cha zimene adzachite. Kenaka iwoŵa adzachita chilichonse chimene afuna. Tiyeni titsikire komweko, tikasokoneze chilankhulo chao kuti asamvane.” Motero Chauta adaŵamwaza anthuwo pa dziko lonse lapansi, ndipo iwowo adaleka kumanga mzindawo. Choncho mzinda umenewo adautcha Babele, chifukwa choti kumeneko Chauta adasokoneza chilankhulo cha anthu onse. Ndipo kuchokera kumeneko adaŵamwaza anthuwo pa dziko lonse lapansi. Nayi mibadwo yofumira mwa Semu: Patangopita zaka ziŵiri chitatha chigumula, Semu ali wa zaka 100, adabereka mwana dzina lake Aripakisadi. Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka zina 500, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. Pamene Aripakisadi anali wa zaka 35, adabereka mwana dzina lake Sela. Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka zina 403, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. Pamene Sela anali wa zaka 30, adabereka mwana dzina lake Eberi. Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka zina 403, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. Eberi ali wa zaka 34, adabereka mwana dzina lake Pelegi. Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka zina 430, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. Pelegi ali wa zaka 30 adabereka mwana dzina lake Reu. Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka zina 209, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. Reu ali wa zaka 32, adabereka mwana dzina lake Serugi. Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka zina 207, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. Serugi ali wa zaka 30, adabereka mwana dzina lake Nahori. Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka zina 200, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. Nahori ali wa zaka 29, adabereka mwana dzina lake Tera. Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka 119, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. Tera ali wa zaka 70, adabereka Abramu, Nahori ndi Harani. Nazi zidzukulu za Tera: Tera adabereka Abramu, Nahori ndi Harani. Harani adabereka Loti. Haraniyo adafera m'mudzi wa kwao dzina lake Uri, wa ku Kaldeya. Adafa atate ake akali moyo. Abramu ndi Nahori adakwatira. Abramu adakwatira Sarai, ndipo Nahori adakwatira Milika mwana wa Harani, amene analinso bambo wake wa Isika. Sarai analibe ana chifukwa anali wosabala. Tsono Tera adatenga mwana wake Abramu ndi Loti mdzukulu wake, mwana wa Harani, ndiponso mpongozi wake Sarai, mkazi wa Abramu. Adanyamuka ulendo kuchoka ku mzinda uja wa Uri wa ku Kaldeya napita nawo ku dziko la Kanani. Adakafika ku Harani, nakhazikika kumeneko. Ndipo Tera adafera kumeneko ali wa zaka 205. Tsiku lina Chauta adauza Abramu kuti, “Choka kudziko kwako kuno. Usiye abale ako ndi banja la bambo wako, ndipo upite ku dziko limene nditi ndikusonyeze. Ndidzakusandutsa kholo la mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa ndi kukusandutsa wotchuka, kotero kuti udzakhala ngati dalitso kwa anthu ena. “ Ndidzadalitsa onse okudalitsa iwe, koma ndidzatemberera aliyense wokutemberera. Mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzapeza madalitso kudzera mwa iwe.” Abramu anali wa zaka 75 pamene ankachoka ku Harani monga Chauta adaamlamulira, ndipo Loti adapita naye limodzi. Abramu adatenga mkazi wake Sarai, Loti mwana wa mng'ono wake, pamodzi ndi chuma chake chonse, ndi antchito amene adaali nawo ku Harani. Adayamba ulendo wonka ku Kanani. Atafika ku Kanani, Abramuyo adayendera dziko lonselo mpaka adakafika ku Sekemu, ku mtengo wa thundu wa ku More. Pa nthaŵi imeneyo nkuti Akanani akadalimo m'dzikomo. Chauta adaonekera Abramu namuuza kuti, “Dziko limeneli ndidzapatsa zidzukulu zako.” Choncho pa malo amenewo Abramu adamanga guwa, kumangira Chauta amene adaamuwonekera. Pambuyo pake adasendera ku mapiri a kuvuma kwa Betele, ndipo adamanga hema lake pakati pa Betele chakuzambwe ndi Ai chakuvuma. Kumenekonso adamangako guwa, ndipo adatama dzina la Chauta mopemba. Adapitirira ulendo wake pang'onopang'ono, kuloŵera ku Negebu, chigawo chakumwera. Koma m'dziko limenelo mudagwa njala. Ndipo chifukwa choti njala idaakula kwambiri, Abramu adapitirira ndithu chakumwera, mpaka kukafika ku Ejipito, nakhala kumeneko kanthaŵi. Pamene anali pafupi kuwoloka malire a Ejipito, adauza mkazi wake Sarai kuti, “Ndikudziŵa kuti iwetu ndiwe mkazi wokongola. Ndipo Aejipito akakupenya, aziti, ‘Ameneyu ndi mkazi wake,’ tsono kuti akukwatire iwe, andipha ineyo. Chonde, uzikaŵauza kuti, ‘Ndi mlongo wanga.’ Motero zonse zidzandiyendera bwino chifukwa cha iwe, ndipo ndidzapulumuka.” Abramu ataoloka malire kuloŵa mu Ejipito, Aejipito adaonadi kuti mkazi wake ndi wokongola kwambiri. Akalonga a mfumu ya ku Ejipito atamuwona mkaziyo, adakauza Farao za kukongola kwake. Pomwepo anthu aja adamtenga mkaziyo kukamuika ku nyumba ya mfumu. Ndipo Farao adamchitira zabwino Abramu uja chifukwa cha mkaziyo, nampatsa nkhosa, mbuzi, ng'ombe, abulu, ngamira ndiponso akapolo aamuna ndi aakazi. Koma Chauta adagwetsa nthenda zoopsa pa Farao ndi pa anthu a m'nyumba mwake omwe, chifukwa cha Sarai mkazi wa Abramu. Apo Farao adaitana Abramu namufunsa kuti, “Kodi iwe, wandichita zotani? Bwanji osandiwuza kuti ameneyu ndi mkazi wako? Bwanji umanena kuti ndi mlongo wako kuti ine ndimukwatire? Nayu mkazi wako. Mtenge, ndipo uchoke!” Farao adalamula anthu ake, ndipo iwowo adatulutsa Abramu ndi mkazi wake m'dzikomo, pamodzi ndi zonse zimene anali nazo. Abramu ndi mkazi wake atachoka ku Ejipito, adapita ku Negebu, chigawo chakumwera. Ndipo Loti adapita nawo limodzi. Abramu anali wolemera kwambiri. Anali ndi zoŵeta monga: nkhosa, mbuzi ndi ng'ombe, ndiponso siliva ndi golide yemwe. Kuchokera kumwera adasendera ndithu cha ku Betele, ku malo aja kumene kale adaamangako hema lake, pakati pa Betele ndi Ai. Tsono adabwereranso ku malo aja kumene kale adaamangako guwa, ndipo adatama dzina la Chauta mopemba. Loti nayenso amene ankayenda limodzi ndi Abramu, anali ndi nkhosa, mbuzi ndi ng'ombe pamodzi ndi banja lake ndi antchito ake amene ankakhala naye limodzi. Tsono dziko lodyetsapo zoŵeta linali losakwanira onse aŵiriwo, poti aliyense anali ndi zoŵeta zambiri. Motero padaauka ndeu pakati pa abusa a Abramu ndi abusa a Loti. Nthaŵi imeneyo nkuti Akanani ndi Aperizi akadalipo m'dzikomo. Tsono Abramu adauza Loti kuti, “Ifetu ndife abale, choncho pasakhale kukangana pakati pa iwe ndi ine, ndipo abusa ako sayenera kumakangana ndi abusa anga. Tiye tisiyane, usankhe dera lina lililonse la dziko lino limene ufuna. Iwe ukapita kwina, inenso ndipita kwina.” Motero Loti atayang'anayang'ana, adaona kuti chigwa chonse cha mtsinje wa Yordani mpaka ku Zowari chili ndi madzi ambiri. Chigwacho chinali ngati munda wa Chauta kapenanso ngati dziko la Ejipito. Nthaŵi imeneyi nkuti Chauta asanaononge mizinda ya Sodomu ndi Gomora. Loti adadzisankhira chigwa chonse cha Yordani, napita kukakhala chakuvuma. Umu ndimo m'mene anthu aŵiriwo adasiyanirana. Abramu adakhala m'dziko la Kanani, koma Loti adakhazikika pakati pa mizinda yam'chigwa, nakamanga hema pafupi ndi mzinda wa Sodomu. Anthu amumzindawo anali oipa kwambiri, ndipo ankachimwira Chauta. Loti atachoka, Chauta adauza Abramu kuti, “Uyang'ane bwino kumpoto, kumwera, kuvuma ndi kuzambwe. Ndidzakupatsa dziko lonse limene ukuliwonalo, iweyo pamodzi ndi zidzukulu zako. Ndipo lidzakhala lako mpaka muyaya. Ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adzathe kudzaziŵerenga. Yekhayo amene angaŵerenge fumbi la pa dziko lapansi, ndiye adzathe kuŵerenga zidzukulu zakozo. Nyamuka tsopano, uyendere dziko lonselo, chifukwa ndakupatsa,” Motero Abramu adazula hema lake, nakakhala patsinde pa mitengo ya thundu ya ku Mamure, imene ili ku Hebroni. Ndipo kumeneko adamangira Chauta guwa. Masiku amenewo, Amurafere mfumu ya ku Sinara, Ariyoki mfumu ya ku Elasara, Kedorilaomere mfumu ya ku Elamu, ndi Tidala mfumu ya ku Goimu, onseŵa adasonkhana kuti athire nkhondo mafumu asanu aŵa: Mfumu Bera wa ku Sodomu, mfumu Birisa wa ku Gomora, mfumu Sinabe wa ku Adima, mfumu Semebera wa ku Zeboimu ndi mfumu ya ku Bela (ndiye kuti Zowari). Mafumu asanu ameneŵa adasonkhana pamodzi ndi ankhondo ao onse m'chigwa cha Sidimu, (ku Nyanja Yakufa). Kedorilaomere ndiye ankalamulira onseŵa pa zaka khumi ndi ziŵiri, koma chaka chakhumi ndi chitatu onseŵa adamuukira. Pa chaka chakhumi ndi chinai Kedorilaomere pamodzi ndi anzake ogwirizana nawo, adadza ndi nkhondo nagonjetsa Arefaimu amene ankakhala ku Asiteroti-karanaimu, Azuzimu amene ankakhala ku Hamu, ndi Aemimu amene ankakhala ku chigwa cha Kiriyataimu. Adagonjetsanso Ahori amene ankakhala m'mapiri a Seiri mpaka ku Eliparani ku malire a chipululu. Ndipo adapotoloka, nakafika ku Enimisipati (ndiye kuti Kadesi), ndipo adagonjetsa dziko lonse la Aamaleke pamodzi ndi la Aamori amene ankakhala ku Hazazoni-Tamara. Tsono mafumu a ku Sodomu, Gomora, Adima, Zeboimu ndi Bela adasonkhanitsa ankhondo ao m'chigwa cha Sidimu, nalimbana ndi Kedorilaomere wa ku Elamu, Tidala wa ku Goimu, Amurafere wa ku Sinara ndi Ariyoki wa ku Elasara, mafumu asanu kulimbana ndi mafumu anai. Chigwa cha Sidimu chinali chodzaza ndi maenje a phula. Tsono anthu a ku Sodomu ndi Gomora adagonja nathaŵa nkhondo, ndipo adagwa m'maenjemo, koma ena adathaŵira ku mapiri. Mafumu anai aja adatenga zonse za ku Sodomu ndi za ku Gomora, pamodzi ndi chakudya, nachokapo. Adamtenganso Loti, mphwake wa Abramu uja, pamodzi ndi zake zonse, chifukwa ankakhala ku Sodomu komweko. Koma munthu wina atapulumuka, adabwera kwa Abramu Muhebri uja, namuuza zonsezi. Abramuyo ankakhala pafupi ndi mitengo ija ya thundu ya ku Mamure, wa fuko la Amoni, mbale wa Esikolo ndi Anere, amene ankagwirizana ndi Abramu pa nkhondo. Abramu atamva kuti mbale wake wagwidwa, adasonkhanitsa anthu ake odziŵa kumenya nkhondo. Onse pamodzi analipo 318, ndipo adalondola mafumu aja njira yonse mpaka ku Dani. Atafika kumeneko, adagaŵa anthu ake m'magulu, ndipo iye ndi anthu ake adakamenyana nawo ndi usiku mpaka kuŵagonjetseratu. Adaŵapirikitsa mpaka ku Hoba, kumpoto kwa Damasiko, ndipo adaŵalanda zao zonse. Adabwera naye Loti, mwana wa mbale wake, pamodzi ndi zake zonse, kuphatikizapo akazi ndi anthu ena onse. Pamene Abramu ankabwera kuchokera kumene adakagonjetsa Kedorilaomere ndi mafumu ena ogwirizana naye aja, mfumu ya ku Sodomu idatuluka kukakumana naye ku Chigwa cha Save (ndiye kuti Chigwa cha Mfumu). Ndipo Melkizedeki, mfumu ya ku Salemu, wansembe wa Mulungu Wopambanazonse, adabwera kwa Abramu atatenga buledi ndi vinyo. Adadalitsa Abramuyo, adati, “Mulungu Wopambanazonse, Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi, akudalitse iwe Abramu. Atamandike Mulungu Wopambanazonse, amene adakupatsa mphamvu zogonjetsera adani ako onse.” Pamenepo Abramu adapereka kwa Melkizedeki chigawo chachikhumi cha zinthu zonse zimene adaalanda. Komanso mfumu ya ku Sodomu idapempha Abramu kuti “Zinthu zonse mudatengazi, musunge, koma anthu anga okhaŵa mundipatse.” Koma Abramu adayankha kuti, “Ndikulumbira pamaso pa Chauta, Mulungu Wopambanazonse, Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi kuti sindidzatenga zinthu zako mpang'ono pomwe. Sindidzatenga ngakhale mbota kapena chingwe chomangira nsapato, kuti ungamadzanene kuti, ‘Abramu ndidamulemeza ndine.’ Sinditenga kalikonse ai. Nditengako zokhazo zimene anyamata anga adadya, ndi zoyenera kugaŵira amene adandiperekeza, monga Anere, Esikolo ndi Mamure. Iwo atengeko magawo ao.” Zitatha izi, Chauta adaonekera Abramu m'masomphenya namuuza kuti, “Usachite mantha Abramu, Ine ndili ngati chishango chako chokutchinjiriza. Mphotho yako idzakhala yaikulu.” Koma Abramu adati, “Ambuye Chauta, ine ndilibe ana. Tsono mungathe bwanji kundipatsa mphotho? Woloŵa m'malo mwanga ndi Eliyezere wa ku Damasikoyu. Simudandipatse ana, motero mmodzi mwa akapolo anga ndiye amene adzalandire chuma changa kuti chikhale choloŵa chake.” Tsono Chauta adamuuza kuti, “Uyu sadzalandira chuma chako kukhala choloŵa chake. Yemwe adzalandire chuma chakochi ndi mwana wako weniweni.” Pomwepo Chauta adatulutsira Abramu panja, namuuza kuti, “Tayang'ana kuthamboku, ndipo uŵerenge nyenyezizo ngati ungathe. Iwe udzakhala ndi zidzukulu zochuluka ngati nyenyezizo.” Apo Abramu adakhulupirira Chauta, ndipo chifukwa cha chimenecho, Chauta adamuwona kuti ndi wolungama. Tsono Chauta adamuuza kuti, “Ine ndine Chauta amene ndidakutulutsa ku Uri wa ku Kaldeya, kuti ndikupatse dziko lino kuti likhale lakolako.” Koma Abramu adati, “Ambuye Chauta, kodi ndingadziŵe bwanji kuti dziko limeneli lidzakhaladi langa?” Chauta adamuyankha kuti, “Tandipatsa ng'ombe ya zaka zitatu, mbuzi ya zaka zitatu, nkhosa ya zaka zitatu, ndiponso njiŵa ndi nkhunda.” Abramu adabwera nazo nyama zonsezo kwa Mulungu, naziduladula pakati. Adaika mabanduwo aŵiriaŵiri mopenyanapenyana, m'mizere iŵiri. Koma mbalame zija sadazidule. Miphamba idadzatera kuti idye nyama zimene adaaphazo, koma Abramu adaipirikitsa. Pamene dzuŵa linkaloŵa, Abramu adagwidwa ndi tulo tofanato, ndiponso adachita mantha kwambiri. Chauta adamuuza kuti, “Udziŵe ndithu kuti zidzukulu zako zidzakhala alendo m'dziko la eni. Zidzakhala akapolo kumeneko, ndipo zidzazunzika zaka zokwanira 400. Koma mtundu umene udzachite zimenezi, ndidzaulanga, ndipo zidzukulu zakozo potuluka m'dzikomo, zidzatenga chuma chambiri. Tsono iwe udzakhala ndi moyo nthaŵi yaitali ndipo udzafa mwamtendere. Udzaikidwa m'manda utakalamba kwambiri. Patapita mibadwo inai, zidzukulu zakozo zidzabwereranso, chifukwa sindidzaŵathamangitsa Aamori mpaka kuipa kwao kutafika pachimake penipeni kuti adzalangidwe.” Dzuŵa litangoloŵa, kachisisira katagwa, mwadzidzidzi padaoneka mphika wogaduka ndi moto, pamodzi ndi nsakali yoyaka, ndipo ziŵirizi zidadutsa pakati pa nyama zodulidwa zija. Pa tsiku limeneli mpamene Chauta adachita chipangano ndi Abramu nati, “Ndikulonjeza kuti ndidzapatsa zidzukulu zako dziko lonseli kuyambira ku mtsinje wa ku Ejipito mpaka ku mtsinje waukulu wa Yufurate. Ndidzakupatsa dziko la Akeni, la Akenizi, la Akadimoni, la Ahiti, la Aperizi, la Arefaimu, la Aamori, la Akanani, la Agirigasi ndi la Ayebusi.” Sarai mkazi wa Abramu, sadam'balire ana Abramuyo. Koma Sarai anali ndi mdzakazi wake wa ku Ejipito dzina lake Hagara. Tsono Sarai adauza Abramu kuti, “Chauta sadandipatse ana. Bwanji osati muloŵane ndi mdzakazi wangayu kuti kapena nkundibalira mwana?” Abramu adavomereza zimenezo. Motero Sarai adapereka Hagara uja kwa Abramu, kuti akhale mkazi wake wamng'ono. (Zimenezi zidachitika Abramu atakhala ku Kanani zaka khumi). Abramu ataloŵana ndi Hagara, Hagarayo adatenga pathupi ndipo pompo Hagara adayamba kudzitama, namanyoza Sarai. Tsiku lina Sarai adauza Abramu kuti, “Cholakwa chimenechi chakuti Hagara akundinyoza, chili pa inu. Ine ndidakupatsani mdzakazi ameneyu, ndipo kuyambira paja adatenga pathupipa, wakhala akundinyoza. Chauta ndiye aweruze kuti tiwone wolakwa ndani pakati pathu.” Abramu adayankha kuti, “Iyeyu ndi mdzakazi wako, ndipo ali mu ulamuliro wako. Chita naye chilichonse chomwe ufuna.” Choncho Sarai adayamba kuzunza Hagara, mpaka Hagarayo adathaŵa. Mngelo wa Chauta adakumana naye pa chitsime m'chipululu, pa mseu wopita ku Suri. Ndipo adati, “Iwe Hagara, mdzakazi wa Sarai, kodi ukuchokera kuti, nanga ukupita kuti?” Iye adayankha kuti “Ndikuthaŵa mbuyanga Sarai.” Mngelo wa Chautayo adati, “Iyai, bwerera kwa Sarai, ukamgonjere. Ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka, zosaŵerengeka.” Popitiriza mau mngeloyo adati, “Tsopano uli pafupi kukhala ndi mwana wamwamuna, udzamutche Ismaele, ndiye kuti Chauta wamva kulira kwako pa zovuta zako. Koma mwana wako adzakhala ndi mtima wa chilombo, adzadana ndi aliyense, ndipo anthu onse adzadana naye. Adzakhala akudana ndi abale ake onse.” Tsono Hagara adatcha Chauta amene adalankhula naye kuti, “Inu ndinu Mulungu wondipenya,” poti adati, “Pano ndamuwona Iye amene amandipenya.” Nchifukwa chake anthu amachitchula chitsime cha pakati pa Kadesi ndi Beredi kuti Chitsime cha Wamoyo-Wondipenya. Tsono Hagara adamubalira Abramu mwana wamwamuna, namutcha dzina loti Ismaele. Abramu anali wa zake 86 pa nthaŵi imeneyo. Abramu ali wa zaka 99, Chauta adamuwonekera namuuza kuti, “Ine ndine Mulungu Mphambe. Tsono uzindimvera nthaŵi zonse, ndipo uzichita zolungama. Ndidzachita nawe chipangano, ndipo ndidzakupatsa zidzukulu zambiri.” Pomwepo Abramu adagwada pansi ndipo Mulungu adati, “Nachi chipangano chimene ndidzachite nawe. Ndikulonjeza kuti udzakhala kholo la anthu a mitundu yambiri. Dzina lako silidzakhalanso Abramu, koma Abrahamu. Limeneli ndilo dzina lako, chifukwa ndikukusandutsa kholo la anthu a mitundu yambiri. Ndidzakupatsa zidzukulu zambiri, ndipo zina mwa izo zidzakhala mafumu. Udzakhala ndi zidzukulu zambiri kotero kuti zidzakhala mitundu yaikulu. Chipangano changachi ndidzachikhazikitsa pakati pa Ine ndi iwe ndi zidzukulu zako zam'tsogolo, ndipo chidzakhala chipangano chosatha. Ine ndidzakhala Mulungu wako ndi Mulungu wa zidzukulu zako. Dziko lino limene ukukhalamo ngati mlendoli, ndidzakupatsa iwe ndi zidzukulu zako. Dziko lonse la Kanani lidzakhala la zidzukulu zako mpaka muyaya, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao.” Mulungu adauzanso Abrahamu kuti, “Iwenso tsono uyenera kuvomera kusunga chipangano changa, pamodzi ndi zidzukulu zako zam'tsogolo. Iwe pamodzi ndi zidzukulu zako, muyenera kusunga chipangano ichi chakuti mwamuna aliyense pakati panupa aziwumbalidwa. Kuyambira tsopano muziwumbalidwa. Chimenechi chidzakhala chizindikiro cha chipangano pakati pa Ine ndi inu. Muziwumbala mwana wamwamuna aliyense akakwanitsa masiku asanu ndi atatu. Muziwumbala mwamuna aliyense pa mibadwo yanu yonse, mbadwa kapena kapolo amene mudamgula kwa mlendo wosakhala wa mbumba yanu. Inde aliyense aumbalidwe, ndipo chimenechi chidzakhala chizindikiro pa matupi anu, choonetsa kuti chipangano changa ndi inu nchamuyaya. Munthu wamwamuna wosaumbalidwa adzachotsedwa pakati pa anthu a mtundu wake, chifukwa sadasunge chipangano changa.” Pambuyo pake Mulungu adauza Abrahamu kuti, “Mkazi wakoyu usamutchulenso kuti Sarai. Tsopano dzina lake ndi Sara. Iyeyu ndidzamdalitsa ndipo adzakubalira mwana wamwamuna. Ndidzamdalitsa, ndipo adzakhala mai wa mitundu ya anthu. Pakati pa zidzukulu zakezo padzatuluka mafumu.” Apo Abrahamu adagwada pansi. Adayamba kuseka, nati, “Kodi mwamuna woti ali ndi zaka 100, angathe kuberekanso? Kodi Sara, amene ali ndi zaka 90, angathe kubalanso?” Ndipo adauza Mulungu kuti, “Ndikukupemphani kuti mungodalitsa Ismaele yemweyu.” Koma Mulungu adati, “Iyai, ndi mkazi wako Sara amene adzakubalira mwana wamwamuna ndipo udzamutcha Isaki. Ndidzasunga chipangano changa ndi iyeyo ndiponso ndi zidzukulu zake, ndipo chipanganocho chidzakhala chamuyaya. Koma kunena za Ismaeleyu, ndidzamdalitsa, ndipo ndidzampatsa ana ambiri pamodzi ndi zidzukulu. Adzakhala bambo wa mafumu khumi ndi aŵiri, ndipo zidzukulu zake ndidzakhala mtundu waukulu. Koma ndidzasunga chipangano changa ndi mwana wako Isaki amene adzabadwa mwa Sara pa nyengo yonga yomwe ino chaka chamaŵachi.” Mulungu atatha kulankhula ndi Abrahamu, adamsiya pomwepo. Tsiku lomwelo Abrahamu adakumbukira zimene Mulungu adamuuza, ndipo adatenga mwana wake Ismaele ndi akapolo onse obadwira m'nyumba mwake, kapena amene Abrahamu adaŵagula, kungoti amuna onse a m'nyumba mwake, naŵaumbala monga momwe Mulungu adaamuuzira. Abrahamu anali wa zaka 99 pa nthaŵi imene adaumbalidwa. Mwana wake Ismaele anali wa zaka 13 pamene adaumbalidwa. Pa tsiku limeneli Abrahamu ndi mwana wake Ismaele adaumbalidwa, pamodzi ndi anthu aamuna onse, amuna obadwira m'banja mwake ndiponso ena amene adaŵagula ndi ndalama kwa alendo, onsewo adaumbalidwa pamodzi ndi iyeyo. Chauta adaonekera Abrahamu ku mitengo ya thundu ya ku Mamure ija. Abrahamuyo atakhala pa khomo la hema lake nthaŵi yamasana kutatentha, mwadzidzidzi adangoona anthu atatu ataimirira potero. Atangoŵaona, adanyamuka mwamsanga kukaŵalonjera. Adaŵeramitsa mutu, nati, “Mbuyanga, ngati ndapeza kuyanja pamaso panu, chonde musapitirire pakhomo pa mtumiki wanu. Ndikupatseni madzi kuti mutsuke mapazi. Mungathe kubapuma patsinde pa mtengo pano. Ine tsopano ndikatenga chakudya, kuti mukadya mupeze mphamvu zopitirizira ulendo wanu. Mwabwera pakhomo panga pano, motero ndiyenera kukutumikirani.” Anthuwo adayankha kuti, “Chabwino, uchite monga waneneramo.” Abrahamu adaloŵa msangamsanga m'hema, nauza Sara kuti “Utenge msanga nsengwa zitatu za ufa wosalala, uukande ndi kupanga buledi.” Pamenepo Abrahamu adathamanga nakatenga mwanawang'ombe wonenepa, nampereka kwa wantchito kuti akonze mwamsanga. Kenaka adatenga chambiko ndi mkaka wokama chatsopano, ndi nyama yokonzakonza ija naŵapatsa zonsezo. Iye adakhala potero pamene anthuwo analikudya patsinde pa mtengo. Tsono anthuwo adafunsa Abrahamu kuti, “Kodi mkazi wako Sara ali kuti?” Abrahamu adayankha kuti, “Ali m'hemamu.” Chauta adati, “Ndikukulonjeza kuti pakapita miyezi isanu ndi inai ndidzabweranso, ndipo mkazi wako adzakhala ali ndi mwana wamwamuna.” Sara ankangomvetsera ali kuseri kwa chitseko cha hema. Abrahamu pamodzi ndi Sara anali nkhalamba zokhazokha, ndipo nthaŵi imeneyo nkuti Sara ataleka kusamba monga amachitira akazi. Motero Sara adangoseka, namati, “Ha, monga ndakalambira inemu, kodi nkuthekanso kuti ndikondwe ndi mwamuna wanga? Komanso mwamuna wanga ndi wokalamba zedi.” Chauta adafunsa Abrahamu kuti, “Chifukwa chiyani Sara amaseka ndi kunena kuti, ‘Ine monga ndakalambiramu kungatheke bwanji kukhala ndi mwana?’ Kodi chilipo china choti chingakanike Chauta? Tsono pa nthaŵi yake, ndidzachitadi zimene ndalonjezazi, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.” Apo Sara adakana chifukwa cha mantha, adati, “Sindidaseke.” Koma Iye adati, “Inde, unaseka.” Tsono anthuwo adachoka, nafika pamalo pamene anali kupenya Sodomu. Abrahamu adapita nawo limodzi, naŵalozera njira. Ndipo Chauta adanena mwa Iye yekha kuti, “Abrahamuyu sindingamubisire chomwe ndikuti ndichite. Zidzukulu zake zidzakhala mtundu waukulu wamphamvu. Ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadalitsidwa chifukwa cha iye. Ndamsankha iyeyu kuti alamule ana ake ndi mabanja ake akutsogolo kuti azidzamvera mau anga, pochita zabwino ndi zolungama. Choncho ndidzachita zonse zimene ndidamlonjeza.” Tsono Chauta adauza Abrahamu kuti, “Pali zolakwa zoopsa zokhudza Sodomu ndi Gomora, ndipo tchimo lao ndi lalikulu kwambiri. Choncho ndikuti nditsikireko kuti ndikaone ngati zolakwa zimene ndamvazo ndi zoona. Ngati si choncho, ndidzadziŵa.” Anthu aja adachoka, napita ku Sodomu, koma Abrahamu adatsarira ndi Chauta. Apo Abrahamu adayandikira kwa Chauta namufunsa kuti, “Kodi monga mudzaonongadi anthu osachimwa pamodzi ndi ochimwa? Nanga patakhala kuti pali anthu 50 osachimwa mumzindamo, kodi mudzaonongabe mzinda wonse? Kodi simudzauleka kuti musunge anthu 50 amenewo? Ndithu simudzaononga anthu osachimwa pamodzi ndi ochimwa. Chimenechi nchosatheka ndipo simungachite. Mukadatero bwenzi anthu osachimwa akulangidwira kumodzi ndi ochima. Kutalitali, Inu simungachite zotere! Kodi Muweruzi wa dziko lonse lapansi nkupanda chilungamo?” Chauta adayankha kuti, “Ndikapeza anthu 50 osachimwa m'Sodomu, ndidzauleka mzinda wonsewo osauwononga, chifukwa cha anthu 50 amenewo.” Abrahamu adalankhulanso, adati, “Chonde, ndalimba mtima pakulankhula nanu chotere, Ambuye. Inetu ndine munthu chabe pamaso panu. Nanga pa chiŵerengero cha 50 pakangopereŵera anthu asanu okha, bwanji? Kodi mudzaononga mzindawo popeza kuti asoŵa asanu okha?” Chauta adayankha kuti, “Ndikapeza anthu 45 olungama, sindidzaononga mzindawo.” Abrahamu adafunsanso kuti, “Nanga pakapezeka anthu olungama 40 okha?” Chauta adayankha kuti, “Ndikapeza anthu 40, sindidzauwononga.” Apo Abrahamu adati, “Chonde ndapota nanu, musapse mtima, Ambuye, tsopano ndifunsanso. Nanga mutapezeka anthu olungama 30?” Chauta adati, “Ndikapeza anthu 30, sindidzauwononga.” Tsono Abrahamu adati, “Ndapota nanu, khululukireni kulimba mtima chotere polankhula ndi Inu Ambuye. Nanga mutapezeka olungama 20?” Chauta adati, “Ndikapeza anthu olungama 20, sindidzauwononga mzindawo.” Abrahamu adati, “Chonde, musandikwiyire Ambuye, koma ndilankhule kamodzi kokhaka. Nanga mutapezeka khumi okha?” Aponso Chauta adati, “Ndikapeza olungama khumi, sindidzauwononga mzindawo.” Chauta atatha kulankhula ndi Abrahamu, adachokapo, Abrahamuyo nkumabwerera kwao. Angelo aŵiri aja adaloŵa m'Sodomumo madzulo ndi kachisisira, Loti atakhala pafupi ndi chipata cha mzindawo. Tsono Lotiyo atangoŵaona anthuwo, adaimirira nakaŵalonjera. Adaŵeramitsa mutu, nati, “Chonde ambuye anga, tiyeni mukafike kunyumba, mukatsuke mapazi ndi kugona komweko. M'maŵa kukacha, mungathe kupitirira ndi ulendo wanu.” Koma iwo adayankha kuti, “Iyai, ife tigona panja mumzinda mommuno.” Loti adaumirirabe kuŵapempha, ndipo pambuyo pake iwo adavomera, napita kunyumba kwa Loti. Tsono Loti adaŵachitira phwando. Adaŵaphikira buledi wosafufumitsa naŵakonzera chakudya chokoma kwambiri, anthuwo nkudya. Alendowo asanakagone, anthu onse amumzindamo, achinyamata ndi okalamba omwe, adadzazinga nyumbayo. Adaitana Loti namufunsa kuti, “Kodi anthu abwera kwanu usiku uno aja ali kuti? Atulutse, abwere kuno kuti tigone nawo.” Loti adatuluka panja natseka chitseko. Tsono adaŵapempha kuti, “Inu abwenzi anga, musachite zimenezi chifukwa nkulakwa kwambiri kuchita zotere. Onani, ine ndili ndi ana aakazi aŵiri, anamwali osadziŵa mwamuna. Bwanji ndikupatseni ana ameneŵa kuti muchite nawo zomwe mukufuna. Koma alendoŵa, musaŵachite kanthu kena kalikonse chifukwa ndi alendo anga, ndipo ndiyenera kuŵatchinjiriza.” Koma iwowo adati, “Choka apa, wakudza iwe! Ndiwe yani iwe kuti ungatiwuze zoti tichite? Tachoka apa! Mwina mwake tingathe kukuzunza kwambiri kupambana iwowo.” Motero adamkankha Lotiyo, nasendera kuti akathyole chitseko. Koma anthu aŵiri anali m'kati aja adamkokera Lotiyo m'nyumba, natseka chitseko. Kenaka adaŵachititsa khungu anthu onse amene adaaima pabwalowo, achinyamata ndi okalamba omwe, kotero kuti sadathenso kuwona khomo. Anthu aŵiriwo adafunsa Loti kuti, “Kodi aliponso wina aliyense amene uli naye kuno? Tenga ana ako aamuna, ana ako aakazi, akamwini ako ndi wina aliyense wachibale amene ali mumzinda muno, mutuluke, chifukwa ife tikuti tiwononge malo ano. Chauta waziona zoipa zonse zimene anthu okhala mumzinda muno akuchita, ndipo tatumidwa kuti tiuwononge mzindawu.” Pamenepo Loti adapita kwa anyamata amene ankafuna kukwatira ana akewo naŵauza kuti, “Fulumirani, tiyeni tituluke kuno, chifukwa patsala pang'ono kuti Chauta aononge malo ano.” Koma iwowo ankangoyesa nthabwala chabe. M'mamaŵa, angelo aja adayesa kumufulumizitsa Loti namuuza kuti, “Fulumira! Iweyo ndi mkazi wako ndi ana ako aakazi aŵiri, mutuluke kupita kunja kwa mzinda, kuti mupulumutse moyo wanu pamene mzinda uno ukukaonongedwa.” Koma Loti ankakayikabe, tsono Chauta adamumvera chifundo. Motero anthuwo adatenga Loti, mkazi wake ndi ana ake aŵiri aja moŵagwira pa dzanja, naŵatulutsa mumzindamo, nkuŵasiya panja pomwepo. Ataŵatulutsira kunja kwa mzindawo, mmodzi mwa angelowo adati, “Thamangani, mupulumutse moyo wanu. Musacheukire m'mbuyo, ndipo musaime m'chigwamo. Thaŵirani ku mapiri kuti mungaphedwe.” Koma Loti adamuyankha kuti, “Iyai mbuyanga musatero. Mwandikomera mtima kwambiri pakupulumutsa moyo wanga. Komatu mapiriwo ali patali kwambiri. Kuwonongeka kwa malo ano mwanenaku kuchitika ine ndisanafike kumapiriko, ndipo ndifa. Apo patsidyapo pali kamzinda kakang'ono. Pamenepo mpafupi, ndingathe kukafika. Bwanji ndipite kumeneko. Nkochepa kwambiri, koma ndikhoza kupulumukirako.” Munthuyo adayankha kuti, “Zimenezo ndavomereza. Kamzinda kameneko sindikaononga. Fulumira! Thamanga! Sindichita kena kalikonse mpaka iwe utafika kumeneko.” Choncho Loti adathamanga nakafika ku kamzinda kaja. Nchifukwa chake kamzindako adakatcha Zowari. Pamene dzuŵa linkatuluka, Loti nkuti atafika kale ku Zowari. Tsono Chauta adagwetsa moto wa sulufule pa Sodomu ndi Gomora kuchokera kumwamba. Motero adaonongeratu mizinda imeneyi, pamodzi ndi chigwa chonse ndi anthu onse am'mizindamo, kuphatikizapo zomera zonse za m'dziko limenelo. Koma mkazi wa Loti adaacheukira m'mbuyo, ndiye pomwepo adasanduka mwala wamchere. M'maŵa mwake, m'mamaŵa, Abrahamu adathamangira ku malo omwe aja, kumene adaaimirira pamaso pa Chauta. Adayang'ana ku mizinda ya Sodomu ndi Gomora ndi ku chigwa chija. Ndipo adangoona utsi uli tolotolo kutuluka m'chigwamo ngati utsi wotuluka m'ng'anjo ya moto. Motero pamene Chauta ankaononga mizinda yam'chigwayo, adakumbukira pemphero la Abrahamu, ndipo adapulumutsa Loti ku chiwonongeko chimene chidasakaza mizinda ija m'mene Loti ankakhala. Popeza kuti Loti ankaopa kukhala ku Zowari, iyeyo pamodzi ndi ana ake aakazi aŵiri aja, adapita ku dziko lamapiri, onsewo nkumakakhala m'mapanga. Mwana wamkulu adauza mng'ono wake kuti, “Bambo athuŵa akukalamba tsopano, ndipo palibe munthu ndi mmodzi yemwe pa dziko lapansi woti angatikwatire, kuti tibale ana monga momwe zimachitikira zinthu pa dziko lapansi. Tiye tiŵaledzeretse abamboŵa kuti agone nafe, kuti mtundu usathe. Choncho usiku womwewo anawo adampatsa vinyo bambo waoyo. Zitatero, mwana wamkuluyo adagona ndi bambo wake. Pamenepo nkuti bamboyo ataledzera kwambiri, kotero kuti sankadziŵa zimene zinkachitika.” M'maŵa mwake mwana wamkuluyo adauza mng'ono wake uja kuti, “Ine dzulo ndidagona ndi atate. Tiye tsono tiŵaledzeretsenso kuti iwenso ugone nawo, kuti choncho mtundu wathu usathe.” Motero usiku umenewo adamledzeretsanso, ndipo mwana wamng'onoyo adagona ndi bambo wake. Nthaŵi imeneyinso nkuti bamboyo ataledzera, kotero kuti sadadziŵe zochitikazo. Mwa njira imeneyi, ana onse aŵiriwo a Loti adatenga pathupi pa bambo wao. Mwana wamkuluyo adabala mwana wamwamuna, namutcha Mowabu. Iyeyo ndiye kholo la Amowabu onse. Mwana wamng'onoyo nayenso adabala mwana wamwamuna, namutcha Benami. Iyeyo ndiye kholo la Aamoni. Abrahamu adachokako ku Mamure kuja napita ku Negebu, chigawo chakumwera. Adakakhala pakati pa mzinda wa Kadesi ndi dziko la Suri, nakhazikika ku dziko la Gerari. Kumeneko adauza anthu kuti, “Sarayu ndi mlongo wanga.” Motero Abimeleki, mfumu ya ku Gerari, adamtenga Sarayo. Tsono Mulungu adamuwonekera usiku m'maloto nati, “Ufatu iwe chifukwa mkazi watengayu ndi wokwatiwa.” Koma Abimeleki anali asanamkhudze mkaziyo, choncho adati, “Ambuye, kodi Inu mungaphedi munthu wosalakwa? Abrahamu pondiwuza adati, ‘Ndi mlongo wanga,’ ndipo iyenso mwini wake ankanena kuti, ‘Ndi mlongo wanga.’ Ine pochita zimenezi, mtima wanga sudanditsutse konse, ndipo sindidalakwe.” Mulungu adamuyankha m'maloto momwemo kuti, “Inde ndikudziŵa kuti iwe udachita zimenezi popanda mtima wako kukutsutsa. Choncho ndidakuletsa ndine kuti usandichimwire pakumkhudza mkaziyo. Koma tsopano, umpereke mkazi ameneyu kwa mwamuna wake. Mwamunayo ndi mneneri, ndipo adzakupempherera kuti usafe. Koma ukapanda kumpereka, ndikukuchenjezeratu kuti udzafa ndithu, iweyo ndi banja lako lonse.” M'maŵa mwake, m'mamaŵa, Abimeleki adaitana antchito ake onse naŵauza zonsezi, ndipo anthuwo adachita mantha kwambiri. Tsono Abimeleki adaitana Abrahamu namufunsa kuti, “Kodi iwe watichita zotani? Kodi ine ndakulakwira chiyani, kuti iweyo undiputire chilango chotere ine ndi onse a mu ufumu wanga? Zimene wandichitazi nzosayenera konse kuzichita. Chifukwa chiyani wachita zimenezi?” Abrahamu adayankha kuti, “Ndinkaganiza kuti kuno kulibe ndi mmodzi yemwe woopa Mulungu, ndipo kuti akadandipha nkutenga mkazi wangayu. Komabetu, kunena zoona, ndi mlongo wangadi ameneyu, chifukwa ndi mwana wa bambo wanga, koma osati womubala mai wanga, ineyo nkumukwatira. Motero pamene Mulungu adandituma kuchokera kunyumba kwa bambo wanga, kuti ndipite ku maiko achilendo, ndidaamuuza mkazi wangayu kuti, ‘Undiwonetse kuti ndiwedi wokhulupirika kwa ine, pouza aliyense kuti ndine mlongo wako, kulikonse kumene tizipita.’ ” Tsono Abimeleki adabwezera Sara kwa Abrahamu, ndipo nthaŵi yomweyo adampatsa nkhosa, ng'ombe ndi akapolo aamuna ndi aakazi. Adauza Abrahamu kuti, “Dziko lonseli ndi langa, ungathe kukhala kulikonse komwe ukufuna.” Ndipo adauza Sara kuti, “Mlongo wakoyu ndikumpatsa ndalama zasiliva chikwi chimodzi, kuti zikhale ngati mboni kwa onse amene ali nawoŵa kuti iwe ndiwe wosalakwa.” Motero Abrahamu adapempherera Abimeleki, ndipo Mulungu adamchiza. Adachizanso mkazi wake pamodzi ndi antchito ake aakazi, kuti onsewo azitha kubala. Ndiye kuti Chauta anali ataŵatseka akazi onse a m'banja la Abimeleki kuti akhale osabala, chifukwa cha Sara mdzakazi wa Abrahamu. Chauta adakumbukira Sara namchitira zimene adaamulonjeza. Choncho Sarayo adatenga pathupi, nabalira Abrahamu mwana wamwamuna pamene Abrahamuyo anali nkhalamba. Mwana ameneyu adabadwa pa nthaŵi yeniyeni imene Mulungu adaanena. Ndipo mwana wa Abrahamuyo, mwana amene Sara adamubalirayo, Abrahamu adamutcha Isaki. Abrahamu adamuumbala mwanayo ali wa masiku asanu ndi atatu, monga momwe Mulungu adaalamulira. Abrahamu nkuti ali wa zaka 100 pamene Isakiyo adabadwa. Tsono Sara adati, “Mulungu wandikondweretsa ndi kundiseketsa. Aliyense amene adzamve zimenezi, adzakondwera nane.” Ndipo adati, “Akadadziŵa ndani kuti Sara nkuyamwitsa mwana? Komabe ndamubalira mwana wamwamuna Abrahamu pamene ali nkhalamba.” Mwanayo adakula, ndipo pa tsiku lakuti amuletsa kuyamwa, Abrahamu adachita phwando lalikulu. Tsiku lina Ismaele, amene Hagara Mwejipito uja adabalira Abrahamu, ankamunyoza Isaki mwana wa Sara. Sara ataona, adauza Abrahamu kuti, “Mchotseni mdzakaziyu pamodzi ndi mwana wake yemweyu. Mwana wa mdzakazi asadzalandireko chuma chanu chimene adzalandire mwana wanga Isaki.” Zimenezi zidamuvuta kwambiri Abrahamu, chifukwa chakuti Ismaele nayenso anali mwana wake. Koma Mulungu adauza Abrahamu kuti, “Mtima wako usavutike chifukwa cha mwanayo ndi mzikazi wako Hagara. Zonse zimene akukuuza Sara uchite, chifukwa Isakiyu ndi amene adzakhala kholo la zidzukulu zako monga momwe ndidakulonjezera. Mwana wa mdzakaziyunso ndidzampatsa ana ambiri, ndipo adzasanduka mtundu ndithu, popeza kuti iyeyunso ndi mwana wako.” M'maŵa mwake, m'mamaŵa, Abrahamu adapatsa Hagara chakudya ndi thumba lachikopa la madzi. Kenaka adatenga mwanayo nabereketsa Hagara, ndipo atatero adamuuza kuti azipita. Hagara adachokadi, nkumangoyendayenda m'chipululu cha Beereseba. Tsono madzi aja atamthera, adangosiya mwanayo pa chitsamba. Iye adakakhala pansi poteropo, pa mtunda wa mamita 100, chifukwa ankati, “Ine sindingathe kumaonerera mwana wanga alikufa chotere.” Ali pansi pomwepo, mwanayo adayamba kulira. Mulungu adamumva mwanayo akulira, ndipo mngelo wa Mulungu adalankhula ndi Hagara kuchokera kumwamba, adati, “Kodi iwe Hagara, chikukuvuta nchiyani? Usachite mantha. Mulungu wamva kulira kwa mwanayu. Dzuka, pita, ukamnyamule ndi kumgwiritsa ndi dzanja lako. Zidzukulu zako zidzakhala mtundu waukulu.” Apo Mulungu adatsekula maso a Hagara, ndipo adaona chitsime. Iye adapita pachitsimepo, nakadzaza thumba lachikopa lija ndi madzi, nkumwetsako mwanayo. Mulungu adakhala naye mwanayo mpaka kukula. Adakulira m'chipululu cha Perani, nasanduka katswiri wa uta. Mai wakeyo adampezera mkazi wa ku Ejipito. Pa nthaŵi imeneyo Abimeleki, pamodzi ndi Fikolo, mkulu wa gulu lake la ankhondo, adapita kwa Abrahamu kukamuuza kuti, “Inu, Mulungu ali nanu pa zonse zimene mumachita. Nchifukwa chake tsono, lumbirani pano pamaso pa Mulungu kuti simudzandinyenga ineyo, kapena ana anga, kapenanso zidzukulu zanga. Ine ndakhala wokhulupirika kwa inu, ndiye inunso mulonjeze kuti mudzakhala wokhulupirika kwa ine, m'dziko limene mukukhalamolo.” Abrahamu adati, “Ndikulumbira.” Pambuyo pake Abrahamu adamdandaulira Abimeleki za chitsime chimene antchito ake adaalanda. Abimeleki adati, “Sindikudziŵa amene adachita zimenezi. Ngakhale inu nomwe simudandiwuze, ndipo ine kumva nkomweku.” Abrahamu adapatsa Abimeleki nkhosa ndi ng'ombe, ndipo onse aŵiriwo adachita chipangano. Abrahamu adapatulako anaankhosa asanu ndi aŵiri kuchotsa pa zoŵeta zake. Abimeleki adamufunsa kuti “Chifukwa chiyani mukuchita zimenezi?” Abrahamu adayankha kuti, “Inu landirani nkhosa zisanu ndi ziŵirizi, chifukwa mukatero mukuvomereza kuti chitsimechi ndidakumba ndine.” Motero malo amenewo adatchedwa Beereseba chifukwa kumeneko ndiko kumene anthu aŵiriwo adachita chipangano. Atachita chipangano chimenechi ku Beereseba kuja, Abimeleki ndi Fikolo mkulu wa gulu la ankhondo, adabwerera kwao ku dziko la Afilisti. Tsono Abrahamu adabzala mtengo wa mbwemba ku Beereseba, natama dzina la Chauta, Mulungu Wamuyaya, mopemba. Ndipo adakhala m'dziko la Afilisti nthaŵi yaitali. Pambuyo pake Mulungu adamuyesa Abrahamu. Adamuitana, adati, “Abrahamu!” Ndipo Abrahamu adayankha kuti, “Ee Ambuye.” Mulungu adati, “Tenga Isaki, mwana wako mmodzi yekha uja amene umamkonda kwambiri, upite ku dziko la Moriya. Kumeneko ukampereke ngati nsembe yopsereza pa phiri limene ndidzakuuza.” M'maŵa mwake Abrahamu adakonza chishalo pa bulu wake nadulanso nkhuni zokaotchera nsembe, ndipo adatenga Isaki pamodzi ndi antchito ake aŵiri, nanyamuka ulendo wopita ku malo amene Mulungu adaamuuza. Pa tsiku lachitatu lake Abrahamu adaona malowo chapatali. Ndipo adauza antchito ake aja kuti, “Inu bakhalani pano ndi buluyu. Ine ndi mnyamatayu tipita uko kukapemphera, pambuyo pake tidzakupezani.” Abrahamu adasenzetsa Isaki nkhuni zokaotchera nsembe yopsereza ija, iyeyo adaatenga moto m'manja mwake, pamodzi ndi mpeni, onse nkumayendera limodzi. Tsono Isaki adaitana bambo wake kuti, “Atate.” Abrahamu adavomera kuti, “Ee, mwana wanga.” Isaki adafunsa kuti, “Moto ndi nkhuni ndikuziwona, zilipo, koma nanga mwanawankhosa wokaotchera nsembe ali kuti?” Abrahamu adamuyankha kuti, “Mwana wanga, Mulungu akatipatsa mwanawankhosayo.” Choncho onse aŵiri adapitiriza ulendo wao limodzi. Atafika ku malo amene adaamuuza Mulungu aja, Abrahamu adamanga guwa, naika nkhuni pamwamba pa guwalo. Kenaka adamanga mwana wake uja, namgoneka pamwamba pa nkhunizo. Tsono adasolola mpeni kuti amuphe mwana wakeyo. Koma mngelo wa Chauta adamuitana kuchokera kumwamba, adati, “Abrahamu, Abrahamu!” Iye adayankha kuti, “Ee, Ambuye!” Mngeloyo adati, “Usamuphe mnyamatayo, kapena kumchita kanthu kena kalikonse. Ndikudziŵa kuti ndiwe womveradi Mulungu, chifukwa sudandimane mwana wako mmodzi yekhayo.” Abrahamu atayang'ana, adaona kuti pali nkhosa yamphongo yogwidwa nyanga zake m'ziyangoyango. Adapita kukaigwira, naipha ngati nsembe yopsereza m'malo mwa mwana wake uja. Abrahamu adaŵatcha malowo kuti Chauta adapatsa. Ndipo mpaka lero lino anthu amati, “Paphiri la Chauta adzapatsa.” Mngelo wa Chauta uja adamuitana Abrahamu kachiŵiri kuchokera kumwamba, adati, “Chauta akunena kuti, ‘Ndikulumbira kuti ndidzakudalitsa kwambiri iwe chifukwa wachita zimenezi, osandimana mwana wako mmodzi yekha uja. Ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka ngati nyenyezi zakumwamba, kapenanso ngati mchenga wa m'mbali mwa nyanja. Zidzukulu zakozo zidzagonjetsa adani ao onse. Ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzalandira madalitso kudzera mwa zidzukulu zako, chifukwa iwe wandimvera.’ ” Abrahamu adabwerera kumene adaasiya antchito ake kuja, ndipo onsewo adapita ku Beereseba. Tsono Abrahamu adakhazikika komweko. Pambuyo pake Abrahamu adamva kuti Milika adabalira Nahori mbale wake ana asanu ndi atatu. Mwana wake wachisamba anali Uzi, mng'ono wa Uziyo anali Buzi. Panalinso Kemuwele, bambo wake wa Aramu, Kesedi, Hazo, Pilidasi, Idilafe ndi Betuele. Betuele adabereka Rebeka. Milika adabalira Nahori mbale wa Abrahamu ana asanu ndi atatu ameneŵa. Ndipo Reuma, mzikazi wa Nahori, adabala Teba, Gahamu, Tahasi ndi Maaka. Sara adakhala ndi moyo zaka 127, ndipo adafera ku Kiriyati-Ariba (ndiye kuti Hebroni) m'dziko la Kanani. Abrahamu adapita kumeneko nakalira maliro a Sarayo. Kenaka adasiya mtembo wa mkazi wakewo, nakalankhula ndi anthu a ku Hiti kuti, “Ine ndine mlendo kwanu kuno, wongoyenda. Mundigulitseko kadziko kuti kakhale manda, kuti ndiike mkazi wanga.” Anthuwo adamuyankha kuti, “Timvereni, mbuyathu. Inu ndinu nduna yaikulu pakati pathu pano. Mkazi wanuyu, mumuike m'manda aliwonse abwino amene tili nawo. Palibe ndi mmodzi yemwe pakati pathu pano amene angakumaneni manda amene tili nawo, kapena kukuletsani kuikamo amaiŵa.” Apo Abrahamu adaimirira nkuŵeramira anthuwo, naŵauza kuti, “Ngati mukuvomera kuti ndiike mkazi wangayu kuno, chonde pemphereni Efuroni Muhiti, mwana wa Zohari, kuti andigulitse phanga la Makipera ali naloli. Phangalo lili m'malire a munda wake. Mpempheni kuti andigulitse pa mtengo wake ndithu, inu mukupenya, kuti malowo ndiŵasandutse manda.” Pamenepo nkuti Efuroniyo ali pamodzi ndi Ahiti ku malo ochitirako msonkhano pa chipata cha mudzi. Ndipo anthu onsewo akumva, iye adayankha kuti, “Ai, mbuyanga. Ine ndikupatsani munda wonsewu pamodzi ndi phanga lomweli. Ndikupatsani chabe malowo pamaso pa anthu anga onseŵa, kuti muikemo amai amene atisiyaŵa.” Apo Abrahamu adaŵerama pamaso pa anthu onse aja, nauza Efuroni pakhamu pa onse kuti, “Koma chonde, mundimvere, ine ndichita kugula mundawu. Landirani ndalama za mtengo wake wa mundawu, kuti mkazi wanga ndidzamuike m'menemo.” Koma Efuroni adayankha kuti, “Mvereni, mbuyanga. Malowo mtengo wake ndi masekeli a siliva okwana 400. Koma zimenezo nchiyani pakati pa inu ndi ine? Ikani maliro anu.” Abrahamu adavomera, ndipo pamaso pa anthu onse a ku Hiti adaŵerenga masekeli a siliva okwana 400 amene Efuroni adaatchula, potsata ndalama zomwe anthu amalonda ankagwiritsa ntchito m'dzikomo pa nthaŵi imeneyo. Umu ndimo m'mene kadziko kaja ka Efuroni ka ku Makipera, kuvuma kwa Mamure, kadasandukira ka Abrahamu. Panali munda ndi phanga lokhala m'malire mwa mundawo, pamodzi ndi mitengo yonse yam'mundamo mpaka kukalekeza ku malire ake. Ahiti amene anali pamsonkhanopo adachitira umboni kuti dera lonselo ndi la Abrahamu. Pambuyo pake Abrahamu adaika mkazi wake Sara m'phanga la munda wa ku Makipera kuvuma kwa Mamure, (ndiye kuti Hebroni), m'dziko la Kanani. Motero mundawo pamodzi ndi manda omwewo amene kale adaali a Ahiti, malo onsewo adapatsidwa kwa Abrahamu, ndipo iye adaŵasandutsa manda. Tsopano Abrahamu anali atakalamba, atagonera zaka zochuluka, ndipo Mulungu adaamudalitsa pa zonse zimene ankachita. Tsiku lina adauza wantchito wake wamkulu amene ankayang'anira zinthu zake zonse kuti, “Tandigwira m'kati mwa ntchafu zangamu. Ndikufuna kuti ulumbire pamaso pa Chauta, Mulungu wa dziko lakumwamba ndi dziko lapansi, kuti sudzamufunira mbeta mwana wanga pakati pa atsikana Achikanani kuno ndili ine kuno. Koma udzapita ku dziko lakwathu, ndipo ukamutengera mkazi mwana wanga kumeneko pakati pa abale anga.” Koma wantchitoyo adafunsa kuti, “Nanga zidzatani mkaziyo akadzakana kubwera nane kuno? Kodi mwana wanuyo ndidzamperekeze ku dziko lanu kumene mudachokera?” Abrahamu adayankha kuti, “Usadzamperekeze kumeneko mwana wangayo. Chauta, Mulungu Wakumwamba, adanditenga kwathu m'banja mwa bambo wanga ndi m'dziko limene ndidabadwira, ndipo adandilonjeza molumbira kuti, ‘Dziko lino ndidzapatsa zidzukulu zako.’ Chautayo adzatuma mngelo wake wokutsogolera, ndipo kumeneko udzamutengera mkazi mwana wanga. Koma ngati mkaziyo adzakana kubwera nawe kuno, udzamasuka ku lumbiro limeneli. Komabe mwa njira iliyonse, mwana wanga usadzapite naye kuti akakhale kumeneko.” Motero wantchitoyo adaika dzanja lake m'kati mwa ntchafu za Abrahamu mbuye wake, ndipo adalumbira kuti, “Ndidzachita zonse zimene mwanenazi.” Tsono wantchitoyo adatenga ngamira khumi za mbuye wake, ndi mphatso zambiri zamtengowapatali, ndipo adapita ku mzinda wa Nahori, m'dziko la Mesopotamiya. Atafika, adazigwaditsa pansi ngamirazo pafupi ndi chitsime, kunja kwa mzinda. Anali madzulo ndithu, nthaŵi imene akazi ankabwera kuchitsimeko kudzatunga madzi. Ndipo wantchito uja adayamba kupemphera, adati, “Chauta, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, ndikukupemphani kuti zinthu zitheke lero lino, ndipo muwonetse chikondi chanu chosasinthika chimene muli nacho pa mbuyanga Abrahamu. Ndili pano pa chitsime, ndipo akazi amumzindamu abwera kudzatunga madzi. Ine ndipempha namwali wina kuti, ‘Chonde tatsitsa mtsuko wako kuti ndimweko madzi.’ Tsono namwaliyo akandilola kuti, ‘Imwani, ndipo ndikumwetserani ngamira zanu,’ ameneyo ndiye akhale namwali amene mwasankhira mtumiki wanu Isaki. Zimenezi zikachitika, ndidziŵadi kuti mwamkomera mtima mbuyanga.” Asanamalize nkomwe kupemphera, anangoona uyu, watulukira Rebeka, atasenza mtsuko pa phewa. Iyeyu anali mwana wa Betuele, mwana wa Milika, mkazi wa Nahori, mbale wake wa Abrahamu. Anali namwali wosadziŵa mwamuna aliyense, wokongola kwambiri. Iye adatsikira kuchitsime kuja, natunga madzi mu mtsuko, nkutulukako. Tsono wantchito uja adamthamangira kuti akakumane naye, nampempha kuti, “Chonde mundipatseko madzi a mumtsuko mwanu kuti ndimwe.” Namwaliyo adati, “Imwani mbuyanga,” ndipo mosachedwa adatsitsa mtsuko wake uja pa phewa, naugwirira kuti mlendoyo amwe. Mlendo uja atamwa madziwo, namwaliyo adati, “Ndibwera nawonso madzi, kuti zimwe ngamira zanu mpaka zikwane.” Pompo madzi amumtsukowo adaŵatsanyulira m'chomwera nyama, nabwerera ku chitsime kukatenga madzi ena oti amwetse ngamirazo mpaka zitakwana. Munthu uja anali phee, kuyang'ana zimene ankachita namwaliyo, kuti aone ngati Chauta wadalitsa ulendo wake kapena ai. Namwali uja atamaliza kumwetsa ngamirazo, munthuyo adatulutsa chipini chagolide cholemera theka la sekeli, naveka Rebeka pamphuno pake. Adamuvekanso pamikono pake zigwinjiri ziŵiri zolemera masekeli agolide okwana 100. Kenaka adafunsa namwaliyo kuti, “Kodi atate anu ndani? Tandiwuzani chonde. Kodi alipo malo oti ine ndi anzangaŵa nkugonako usiku uno?” Namwaliyo adayankha kuti, “Ine ndine mwana wa Betuele, mwana wa Nahori, amene adamubalira Milika.” Adapitiriranso kunena kuti, “Chakudya chodyetsa nyamazi chiliko kwathu, ndipo malo oti inu mugoneko aliponso.” Pamenepo munthu uja adaŵerama nkupembedza Chauta, ndipo adati, “Atamandike Chauta, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, amene wasunga mokhulupirika lonjezo lake kwa mbuyanga. Chauta wandilondolera ine ku nyumba ya mbale wake wa mbuyanga.” Tsono namwali uja adathamangira kunyumba kwa mai wake, nafotokozera onse nkhani yonseyo. Apo Labani, mlongo wa Rebekayo, adaonadi chipini chija pamodzi ndi zigwinjiri pa mikono ya mlongo wakeyo. Atamva mlongo wake akusimba zimene munthu uja adaamuuza, Labaniyo adathamangira kuchitsime kumene kunali munthuko. Adakafika pamalo pomwe adaaima wantchito wa Abrahamu, pafupi ndi ngamira zija kuchitsimeko. Adauza munthuyo kuti, “Tiyeni kwathu, inu ndinu munthu amene Chauta wakudalitsani. Bwanji mukuima kuno? Ine ndakukonzerani kale malo kunyumba, ndiponso malo a ngamira zanu.” Motero munthu uja adakaloŵa m'nyumba, ndipo Labani adamasula katundu amene zidaasenza ngamirazo. Atatero adazipatsa chakudya, naŵapatsa madzi alendo onsewo kuti asambe. Chitabwera chakudya, munthu uja adati, “Sindidya konse mpaka nditanena zimene ndadzera.” Apo Labani adamuuza kuti, “Nenani.” Iyeyo adati, “Ine ndine wantchito wa Abrahamu. Chauta adamdalitsa kwambiri mbuyanga, ndipo adamkuza kwambiri. Ali ndi nkhosa ndi mbuzi ndi ng'ombe zochuluka. Alinso ndi siliva ndi golide, akapolo aamuna ndi aakazi, ndiponso ngamira ndi abulu ambiri. Sara, mkazi wake wa mbuyanga, adamubalira mwana wamwamuna, Sarayo atakalamba kale. Ndipo mbuyangayo wamupatsa chuma chake chonse mwana ameneyo. Tsono mbuyanga adandilumbiritsa kuti ndisunge mau ake akuti, ‘Mwana wangayu usadzamfunire mbeta pakati pa anamwali a dziko lino la Kanani, kumene ndili ine kuno. Koma upite kwathu kwa atate anga ndi achibale anga, kukamutengera mkazi mwana wanga kumeneko.’ Ndipo ine ndidamuyankha mbuyanga kuti, ‘Nanga zidzatani ngati mkaziyo adzakana kubwera nane kuno?’ Iye adandiyankha kuti, ‘Chauta amene ndakhala ndikumumvera nthaŵi zonse, adzatuma mngelo wake kuti apite pamodzi nawe, ndipo adzakuthandiza. Udzampezera mkazi mwana wanga pakati pa anthu anga, m'banja la bambo wanga. Ukachita zimenezi, matemberero anga sadzakugwera. Koma iweyo utafika ku banja langalo, anthu angawo nakakukana, udzamasuka ku lumbiro lako.’ “Tsono lero lino nditafika ku chitsime, ndinapemphera kuti, ‘Chauta, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, chonde mundithandize kuti ndikhoze pa ulendo wangawu. Ndili pano pachitsime, pakabwera namwali pano kudzatunga madzi, ine ndidzampempha kuti: Chonde patseko madzi a mumtsuko mwako kuti ndimwe. Iye akandiyankha kuti: Imwani ndipo ndimwetsanso ngamira zanuzi, ameneyo ndiye akhale namwali amene Chauta wamsankha kuti akhale mkazi wa mwana wa mbuyanga.’ Ndisanamalize nkomwe pemphero langalo, ndinangoona uyu, watulukira Rebeka, atasenza mtsuko pa phewa, akutsikira ku chitsime kudzatunga madzi. Tsono ndinampempha kuti, ‘Chonde patseko madzi ndimwe.’ Mosachedwa anatsitsa mtsuko wake pa phewa, nandiwuza kuti, ‘Imwani, ndipo ndimwetsanso ngamira zanuzi.’ Motero ine ndinamwa, ndipo iye anamwetsanso ngamirazo. Ndiye ndinamufunsa kuti, ‘Atate ako ndani?’ Iye anandiyankha kuti, ‘Atate anga ndi Betuele, mwana wa Nahori, amene adamubalira Milika.’ Pamenepo ndinamuveka chipini pa mphuno, ndiponso zigwinjiri pa mikono. Kenaka ndinaŵerama, nkupembedza Chauta. Ndinatamanda Chauta, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, chifukwa cha kunditsogolera bwino kwambiri. Chauta wandifikitsa kwa mbale wake wa mbuyanga, kumene ndapezako mwana wake amene adzakhale mkazi wa mwana wa mbuyanga. Tsopano inu ngati muti mumkomere mtima mbuyanga mokhulupirika, chonde uzeni ndimve. Apo ai, nenaninso, kuti ine ndidziŵe chochita.” Pamenepo Labani ndi Betuele adauza munthuyo kuti, “Popeza kuti zimenezi nzochokera kwa Chauta, ife sitingachitepo kanthu. Nayu, Rebeka ndi ameneyu, mtengeni muzipita naye. Mukampereke kwa mwana wa mbuyanuyo kuti akakhale mkazi wake, monga momwe Chauta adanenera.” Wantchito wa Abrahamu uja atamva mau ao aja, adaŵeramitsa mutu napembedza Chauta. Kenaka adatulutsa zinthu zasiliva ndi zagolide, pamodzi ndi zovala, napatsa Rebeka. Adaperekanso mphatso zamtengowapatali kwa mlongo wake wa Rebekayo ndi kwa mai wake. Wantchitoyo pamodzi ndi anthu amene anali nayewo adadya ndi kumwa, ndipo adagona komweko. Atadzuka m'maŵa, mlendoyo adati, “Loleni ndizibwerera kwa mbuyanga.” Koma mai wake wa Rebeka, pamodzi ndi mlongo wakeyo, adati, “Ai, namwaliyu akhale ndi ife kuno kanthaŵi, osachepera masiku khumi, pambuyo pake ndiye adzapite.” Koma wantchitoyo adati, “Chonde musandichedwetse. Chauta wandithandiza kwambiri pa ulendo wangawu. Loleni tsono ndibwerere kwa mbuyanga.” Apo iwowo adayankha kuti, “Tiyeni timuitane namwaliyo, kuti timve zimene iyeyo anene.” Motero adamuitana Rebeka namufunsa kuti, “Kodi ukufuna kupita naye munthuyu?” Rebekayo adayankha kuti, “Inde, ndipita.” Choncho adamlola Rebeka pamodzi ndi mlezi wake, kuti apite ndi wantchito wa Abrahamu ndi anthu aja omuperekezaŵa. Ndipo adamdalitsa Rebekayo ponena mau akuti, “Iwe mwana wathu, Chauta akudalitse kuti udzakhale mai wa anthu zikwi zambirimbiri. Zidzukulu zako zidzagonjetse mizinda ya adani ao.” Pomwepo Rebeka pamodzi ndi atsikana ake antchito adanyamuka nakakwera ngamira, nkumapita ndi munthu uja. Isaki anali atachoka kuchipululu kumene kunali chitsime cha Wamoyo-Wondipenya chija, kukakhala m'chigawo chakumwera. Tsiku lina madzulo, Isakiyo ankapita nayenda kuthengo, ndipo adaona ngamira zilikudza. Tsono Rebeka ataona Isaki, adatsika pa ngamira yake ija, nafunsa wantchitoyo kuti, “Nanga munthu ali akudza kunoyu ndani?” Wantchito uja adayankha kuti, “Ndiye mbuyanga uja ameneyu.” Motero Rebeka adatenga nsalu, nadziphimba kumaso. Wantchitoyo adamufotokozera Isaki zonse zimene zidaachitika. Tsono Isaki adatenga Rebeka kuti akhale mkazi wake naloŵa naye m'hema mwake. Isaki adamkonda kwambiri Rebekayo, mwakuti zimenezi zidamtonthoza pa imfa ya mai wake ija. Abrahamu adakwatiranso mkazi wina dzina lake Ketura. Ketura adamubalira Zimirani, Yokisani, Medani, Midiyani, Isibaki ndi Suwa. Yokisani adabereka Sheba ndi Dedani, ndipo ana a Dedani anali Aasuri, Aletusi ndi Aleumi. Ana a Midiyani anali Efa, Efera, Hanoki, Abida ndi Elida. Onseŵa anali zidzukulu za Ketura. Abrahamu adasiyira Isaki zonse zimene anali nazo. Koma asanafe adaŵapatsako mphatso ana ake ena aja amene adaŵabereka mwa akazi ake enawo. Onsewo adaŵatumiza ku dziko lakuvuma kuti akakhale kumeneko, kuŵachotsa kwa mwana wake Isaki. Abrahamu adakhala ndi moyo zaka 175. Adamwalira ali nkhalamba yotheratu, atagonera zaka zochuluka. Ana ake aja, Isaki ndi Ismaele, adamuika m'phanga lija la Makipera, m'munda umene kale udaali wa Efuroni mwana wa Zohari wa ku Hiti. Mundawo unali chakuvuma kwa Mamure. Unali munda umene Abrahamu adaagula kwa Ahiti. Abrahamu ndi mkazi wake Sara adaikidwa kumeneko. Atamwalira Abrahamu, Mulungu adadalitsa mwana wake Isaki amene ankakhala pafupi ndi chitsime cha Wamoyo-Wondipenya chija. Nazi zidzukulu za Ismaele, mwana wa Abrahamu amene adamubalira Hagara, mdzakazi wa ku Ejipito uja. Maina a ana a Ismaele ndi aŵa: woyamba anali Nebayoti, pambuyo pake adabereka Kedara, Adibeele, Mibisamu, Misima, Duma, Masa, Hadadi, Tema, Yeturi, Nafisi ndi Kedema. Ameneŵa ndiwo ana a Ismaele malinga ndi midzi yao ndiponso zigono zao. Anali mafumu khumi ndi aŵiri a mafuko osiyana. (Ismaele anali wa zaka 137 pa nthaŵi imene ankamwalira, ndipo adaikidwa m'manda.) Zidzukulu za Ismaeleyo zinkakhala m'dziko la pakati pa Havila ndi Suri, kuvuma kwa Ejipito, pa njira ya ku Asiriya. Zinkakhala molekana ndi zidzukulu zina za Abrahamu. Nayi mbiri ya Isaki mwana wa Abrahamu: Abrahamu adabereka Isaki, ndipo pamene Isaki adakwatira Rebeka mwana wa Betuele Mwaramu wa ku Mesopotamiya, nkuti ali wa zaka makumi anai. Mlongo wa Rebekayo anali Labani, Mwaramu. Tsono poti mkazi wa Isaki anali wosabereka, Isakiyo adapempherera mkazi wake kwa Chauta. Chauta adamva pemphero lake, ndipo Rebeka adatenga pathupi. Koma pamene ana aŵiriwo anayamba kulimbana m'mimba mwake, adati, “Ngati umu ndimo m'mene zikhalire zinthu, ndikhaliranji ndi moyo?” Ndipo adakafunsa Chauta kuti amuyankhe. Chauta adamuuza kuti, “M'mimba mwako muli mitundu iŵiri ya anthu. Udzabereka mafuko a anthu olimbana: mwana wina adzakhala wamphamvu kupambana mnzake, wamkulu adzakhala wotumikira wamng'ono.” Nthaŵi yakuti achire itakwana, Rebeka adabala mapasa. Mwana woyamba kubadwa anali wofiira, ndipo thupi lake lonse linali ngati chovala chaubweya. Motero adamutcha Esau. Pobadwa mng'ono wake, dzanja lake linali litagwira chidendene cha Esau. Motero adamutcha Yakobe. Pamene ana ameneŵa ankabadwa, nkuti Isaki ali wa zaka 60. Anyamatawo adakula ndithu, ndipo Esau adasanduka mlenje wodziŵa kusaka nyama, wokonda kuyendayenda. Koma Yakobe anali wachete, wokonda kukhala kunyumba. Tsono Isaki ankakonda Esau chifukwa ankadya nyama imene Esauyo ankamupatsa akapha. Koma Rebeka ankakonda Yakobe. Tsiku lina Yakobe adaphika nyemba zofiira, Esau nkubwera kuchokera kuthengo. Anali ndi njala zedi, motero adauza Yakobe kuti, “Ine njala yandipha. Patseko nyemba zofiira waphikazi.” (Nchifukwa chake adamutcha Edomu.) Koma Yakobe adayankha kuti, “Uyambe wandipatsa ukulu wako wauchisamba, ndiye ndikupatse zimenezi.” Esau adati, “Chabwino, inetu ndili pafupi kufa. Kodi ukulu wangawo udzandipinduliranji?” Yakobe adati, “Uyambe walumbira kuti ukulu wakowo wandipatsadi.” Apo Esau adalumbira, nagulitsa ukulu wake wauchisamba kwa Yakobe. Apo Yakobe adapatsa Esau buledi pamodzi ndi nyemba zija, ndipo Esau adadya namwera, kenaka adanyamuka nkuchokapo. Motero Esauyo adanyoza ukulu wake wauchisamba. M'dzikomo mudaloŵanso njala kuwonjezera pa imene idaaloŵa pa nthaŵi ya Abrahamu. Ndipo Isaki adapita kwa Abimeleki mfumu ya Afilisti ku Gerari. Tsono Chauta adaonekera Isaki namuuza kuti, “Usapite ku Ejipito, koma ukhale m'dziko limene ndidzakuuza kuti ukhalemo. Khala kuno ndipo Ine ndidzakhala nawe. Ndidzakudalitsa chifukwa ndidzapereka maiko onseŵa kwa iwe ndi kwa zidzukulu zako. Ndidzasunga lumbiro limene ndidachita kwa bambo wako Abrahamu. Ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka monga momwe ziliri nyenyezi zakuthambo, ndipo zidzukulu zakozo ndidzazipatsa maiko onseŵa. Mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzapeza madalitso kudzera mwa zidzukulu zako. Ndidzakudalitsa iwe chifukwa Abrahamu adandimvera, ndipo adatsata malamulo ndi malangizo anga onse.” Motero Isaki adakhala ku Gerari. Anthu akumeneko atafunsa za mkazi wake, Isaki adati, “Ameneyu ndi mlongo wanga.” Ankachita mantha kunena kuti, “Ndi mkazi wanga.” Ankaopa kuti anthu akumenekowo angamuphe ndipo angakwatire Rebeka, popeza kuti anali wokongola kwambiri. Isaki atakhala kumeneko kanthaŵi ndithu, Abimeleki mfumu ya Afilisti adasuzumira pa zenera kuyang'ana kunja, naona Isaki atakumbatira Rebeka. Apo Abimeleki adatuma munthu kukaitana Isaki. Ndipo adati, “Ameneyu ndi mkazi wako ndithu. Bwanji mujamu unkanena kuti ndi mlongo wako?” Iye adayankha kuti, “Ndinkaganiza kuti ndidzaphedwa ndikanena kuti ndi mkazi wanga.” Abimeleki adamufunsa kuti, “Bwanji iwe wachita zotere? Wina mwa anthu angaŵa bwenzi atamfunsira mkazi wako, iweyo ukadatichimwitsa.” Tsono Abimeleki adalamula anthu ake onse kuti, “Musamuchite kanthu munthuyu pamodzi ndi mkazi wake yemwe. Wina aliyense akangotero, aphedwa.” Isaki adabzala mbeu m'dzikomo, ndipo chaka chimenecho adakolola dzinthu dzochuluka koposa, chifukwa Chauta adaamudalitsa. Chuma chake chidanka chichulukirachulukira, ndipo adasanduka munthu wolemera kwambiri. Afilisti adayamba kuchita naye kaduka, chifukwa choti anali ndi nkhosa ndi ng'ombe zambiri, pamodzi ndi akapolo ochuluka. (Anthuwo anali atakwirira zitsime zonse zimene antchito a bambo wake Abrahamu adaakumba, Abrahamuyo adakali ndi moyo.) Tsono Abimeleki adauza Isaki kuti, “Muchoke kuno. Inu ndinu amphamvu kupambana ife.” Motero Isaki adachoka nakamanga mahema m'chigwa cha Gerari nakhazikikako. Kumeneko adafukulanso zitsime zimene anthu adaakumba pa nthaŵi ya Abrahamu bambo wake. Atafa Abrahamuyo, Afilisti adaazikwirira zitsimezo. Isaki adazitcha zitsimezo maina omwewo amene bambo wake ankazitchula. Antchito a Isaki adakumba chitsime m'chigwa, napezamo madzi. Koma abusa a ku Gerari adayamba kukangana ndi abusa a Isaki, ankati, “Madziŵa ndi athu.” Motero chitsimecho Isaki adachitcha Mkangano, chifukwa adakangana naye. Antchito a Isaki aja adakumba chitsime china, ndipo padaukanso mkangano wina pa za chitsime chimenecho. Motero adachitcha Chidani. Adachoka kumeneko, nakakumba chitsime china. Pa chimenechi panalibe mkangano, motero adachitcha Ufulu. Adati, “Tsopano Chauta watipatsa ufulu m'dziko, ndipo tidzalemera kuno.” Patapita nthaŵi, Isaki adachoka napita ku Beereseba. Usiku Chauta adamuwonekera namuuza kuti, “Ine ndine Mulungu wa bambo wako Abrahamu. Usachite mantha poti Ine ndili nawe. Ndidzakudalitsa, ndipo ndidzakupatsa zidzukulu zambiri chifukwa cha mtumiki wanga Abrahamu.” Tsono Isaki adamanga guwa kumeneko, natama dzina la Chauta mopemba, namanga hema lake komweko, ndipo antchito ake adakumba chitsime komweko. Abimeleki adachoka ku Gerari nabwera kudzacheza ndi Isaki pamodzi ndi Ahuzati, nduna yake, ndi Fikolo mtsogoleri wa ankhondo. Tsono Isaki adaŵafunsa kuti, “Kodi chifukwa chiyani mwabwera kuno kudzandiwona, pamene kale mudaandiwonetsa mtima woipa mpaka kundichotsa m'dziko mwanu?” Iwowo adayankha kuti, “Tsopano tikudziŵa kuti Chauta ali nanu, ndipo taganiza zoti inu ndi ife tichite chipangano. Tikufuna kuti inu mulonjeze kuti simudzatichita zoipa, monga ife sitidakuchiteni zoipa. Tidakuchitirani zabwino, ndipo tidakulolani kuti mupite mwamtendere. Tsopano Chauta wakudalitsani.” Isaki adaŵakonzera phwando, ndipo anthuwo adadya ndi kumwa. M'maŵa kutacha, munthu aliyense adalonjeza ndi kulumbira. Kenaka Isaki adaŵaperekeza, ndipo onsewo adachoka mwamtendere, napita. Tsiku limenelo antchito ake a Isaki adabwera kudzamuuza za chitsime chimene iwowo adaakumba. Adati, “Tapeza madzi.” Isaki adachitcha Siba. Nchifukwa chake mzindawo umatchedwa Beereseba mpaka lero lino. Pamene Esau anali wa zaka makumi anai, adakwatira Yuditi mwana wa Beeri Muhiti. Adakwatiranso Basemati, mwana wa Eloni Muhiti. Onseŵa adapezetsa Isaki ndi Rebeka mavuto aakulu. Isaki atakalamba, adachita khungu, mwakuti sankatha kupenya. Tsono adatumiza mau kuti Esau mwana wake wamkulu abwere. Atabwera, Isaki adamuitana kuti, “Mwana wanga!” Iye adavomera kuti, “Ŵaŵa.” Tsono Isakiyo adati, “Ona, ine nkukalamba kuno, ndipo sindidziŵa tsiku loti ndidzafe. Tenga zida zako, uta ndi mivi yomwe, upite ku thengo ukandiphere nyama. Undiphikire chakudya chokoma chija ndimakondachi, ubwere nacho kuno. Nditadya, ndidzakudalitsa ndisanafe.” Rebeka ankangomvetsera pamene Isaki ankalankhula ndi mwana wake Esau. Tsono Esauyo atapita ku thengo kukasaka nyama yoti akapatse bambo wake, Rebeka adauza Yakobe kuti, “Ine ndamva bambo wako akuuza Esau kuti, ‘Ubwere ndi nyama kuno, undiphikire. Nditadya, ndidzakudalitsa pamaso pa Chauta ndisanafe.’ Ndiye iwe mwana wanga, undimvere ndipo uchite zonse zimene ndikuuze. Pita ku khola, ukanditengere timbuzi tiŵiri tonenepa bwino, kuti ndiphike, ndi kukonza chakudya chimene bambo wako amachikonda. Ukapereke chakudyacho kwa bambo wako kuti akadye, ndipo akudalitse asanafe.” Koma Yakobe adauza mai wake kuti, “Mukudziŵa kuti Esau ndi wacheya, koma ine khungu langa ndi losalala. Mwina mwake bambo wanga adzandikhudza, ndipo adzadziŵa kuti ndikumunyenga. Motero m'malo mondidalitsa, adzanditemberera.” Mai wake adayankha kuti, “Mwana wanga, temberero lakelo lidzagwere ine, osati iwe. Iweyo ungochita zimene ndakuuza, kanditengere timbuzito.” Choncho Yakobe adapita kukatenga timbuzito nakapatsa mai wake, ndipo Rebeka adaphika chakudya chimene bamboyo ankachikonda. Pambuyo pake Rebeka adatenga zovala zabwino za Esau zimene ankazisunga m'nyumba, naveka mng'ono wake Yakobe. Adamuvekanso zikopa za tianatambuzi pamikono pake ndiponso pakhosi pake posalala popanda cheya. Ndipo adatenga buledi ndi chakudya chokonza bwino chija, napatsira Yakobe. Yakobe adapita kwa bambo wake, namuitana kuti, “Bambo!” Isaki adafunsa kuti, “Kodi ndiwe mwana wanga uti?” Yakobe adayankha kuti, “Ndine Esau mwana wanu wamkulu, ndipo zija mudaandiwuzazi ndachita. Chonde dzukani, khalani tsonga, mudye nyama ndakutengeraniyi, ndipo mundidalitse.” Apo Isaki adafunsa kuti, “Kodi nyama imeneyi waipeza bwanji msanga chotere, mwana wanga?” Yakobe adayankha kuti, “Chauta, Mulungu wanu, adandithandiza kuti ndiipeze.” Isaki adauza Yakobe kuti, “Tasendera pafupi kuti ndikukhudze, kuti ndidziŵe ngati ndiwedi mwana wanga Esau, kapena ai.” Yakobe adasendera pafupi ndi bambo wake, ndipo bambo wakeyo adamukhudza nati, “Liwuli ndi la Yakobe, koma mikonoyi ndi ya Esau.” Sadamzindikire Yakobe popeza kuti mikono yake inali yacheya ngati ya Esau. Motero adayambapo kumdalitsa. Koma adafunsanso kuti, “Kodi ndiwedi mwana wanga Esau?” Yakobe adayankhanso kuti, “Ndine amene.” Apo Isaki adati, “Bwera nayo kuno nyama yako, kuti ndidye ndipo ndikudalitse.” Yakobe adabwera ndi nyamayo, Isaki nkudya. Yakobe adampatsanso vinyo woti amwe. Tsono bambo wakeyo adati, “Bwera pafupi, udzandimpsompsone, mwana wanga.” Atabwera pafupi kudzampsompsona Isaki adanunkhiza zovala zimene Yakobe adaavala, ndipo pompo adamdalitsa, adati, “Fungo lokoma la mwana wanga lili ngati fungo la zokolola za m'munda umene Chauta adaudalitsa. Mulungu akugwetsere mvula, ndipo minda yako ikhale yobala bwino. Akupatse zakudya ndi zakumwa zambiri. Anthu azikutumikira, mitundu ya anthu izikugwadira. Ukhale wolamulira pakati pa abale ako, zidzukulu za mai wako zizikugwadira. Atembereredwe onse okutemberera, ndipo adalitsidwe onse okudalitsa.” Isaki atamaliza kudalitsako, Yakobe adachokapo. Nthaŵi yomweyo wafika Esau kuchokera kuuzimba kuja. Iyenso adaphika chakudya chabwino kwambiri, nakapereka kwa bambo wake. Esauyo adati, “Chonde bambo dzukani, khalani tsonga, mudye nyama imene ine mwana wanu ndakutengerani, ndipo mundidalitse.” Isaki adamufunsa kuti, “Kodi iwenso ndiwe yani?” Iye adayankha kuti, “Ndine mwana wanu wamkulu Esau.” Pompo Isaki adayamba kunjenjemera thupi lonse, nafunsa kuti, “Nanga uja adapha nyama nkubwera nayo kwa ineyu ndani? Ndadya kale imeneyo, iwe usanabwere. Ndamudalitsa kale, ndipo madalitso amenewo ndi ake mpaka muyaya.” Esau atamva zimenezi, adalira kwambiri ndi mtima woŵaŵa, ndipo adati, “Bambo, pepani inenso mundidalitseko.” Koma Isaki adayankha kuti, “Mng'ono wako anabwera, ndipo wandinyenga. Iyeyo ndiye amene watenga madalitso ako onse.” Pamenepo Esau adati, “Kameneka nkachiŵiri kundichenjeretsa iye uja. Nchosadodometsa kuti dzina lake ndi Yakobe. Ukulu wanga wauchisamba adandilanda, ndipo tsopano wandilandanso madalitso anga. Kodi monga madalitsowo simudandisungireko ndi pang'ono pomwe?” Isaki adayankha Esauyo kuti, “Ndamudalitsa kale iyeyo kuti akhale mbuyako, ndipo abale ake onse ndaŵasandutsa atumiki ake. Ndampatsa chakudya ndi chomwera chake. Nanga tsopano chatsalanso nchiyani choti ndikuchitire iwe mwana wanga?” Esau adapitirirabe kumpempha bambo wakeyo kuti, “Kodi bambo, dalitso muli nalo limodzi lokhali? Tandidalitsaniko nanenso bambo.” Ndipo atatero adayambanso kulira. Tsono Isaki, bambo wakeyo, adamuuza kuti, “Pa malo ako okhalapo sipadzakhala konse chonde, mvula siidzagwa pa minda yako. Ntchito yako idzakhala yomenya nkhondo, ndipo udzakhala wotumikira mbale wako. Koma ukadzatha kudzimasula, udzachokeratu m'goli la ulamuliro wake.” Motero Esau adadana naye Yakobe chifukwa choti m'malo modalitsa iyeyo, bambo wake adadalitsa Yakobe. Ndipo adati, “Nthaŵi yakuti ndilire maliro a bambo wanga ili pafupi, pamenepo ndidzamupha Yakobeyu.” Koma Rebeka atamva za maganizo onse a Esau, adaitana Yakobe namuuza kuti, “Taona, mbale wako Esau akuganiza zoti akuphe kuti akulipsire. Tsopano mwana wanga, uchite zimene ndikuuze. Konzeka, thaŵira kwa mlongo wanga Labani ku Harani. Bakakhala kwa iyeyo kanthaŵi ndithu, mpaka mtima wa mbale wako utatsika ndi kuiŵala zonse zimene wamchitazi. Pa nthaŵiyo, ine ndidzatuma munthu kudzakutenga. Nanga nditayirenji inu ana anga aŵiri pa tsiku limodzi?” Rebeka adauza Isaki kuti, “Akazi Achihitiŵa, ine ndatopa nawo! Yakobenso akakwatira wina mwa a Ahiti akunoŵa, ine kodi moyo wanga nkukomanso?” Pamenepo Isaki adaitana Yakobe namdalitsa, ndipo adamlamula kuti, “Usakwatire mkazi wa kuno ku Kanani. Konzeka, upite ku Mesopotamiya, kwao kwa Betuele, bambo wa mai wakoyu. Kumeneko ukakwatire mmodzi mwa ana aakazi a Labani, mlongo wa mai wako. Mulungu Mphambe adalitse ukwati wako, ndipo akupatse ana ochuluka, kuti udzakhale gulu lalikulu la mitundu yambiri ya anthu. Akudalitse iwe pamodzi ndi zidzukulu zako monga momwe adadalitsira Abrahamu, kuti lidzakhale lakodi dziko limene ukakhalemolo, dziko limene adapatsa Abrahamu.” Atatero Isaki adatumiza Yakobe ku Mesopotamiya kwa Labani, mwana wa Betuele Mwaramu. Labani anali mlongo wa Rebeka mai wa Yakobe ndi Esau. Esau adamva kuti Isaki wadalitsa Yakobe, ndipo kuti Yakobeyo watumizidwa ku Mesopotamiya kuti akakwatire kumeneko. Adamvanso kuti pomudalitsapo, adamlamula kuti asadzakwatire mkazi wa ku Kanani. Adamva kuti Yakobe wamvera bambo wake ndi mai wake, ndipo kuti wapita ku Mesopotamiya. Pamenepo Esau adadziŵa kuti bambo wake Isaki sankaŵakonda akazi a ku Kanani. Motero adapita kwa Ismaele mwana wa Abrahamu, nakwatira Maharati mwana wa Ismaele, mlongo wa Nebayoti. Yakobe adanyamuka ulendo kuchoka ku Beereseba, kupita ku Harani. Atafika pamalo pena, adaima pamenepo chifukwa dzuŵa linali litaloŵa. Adagona pompo atatsamira mwala. Ndipo adalota akuwona makwerero ochoka pansi mpaka kukafika kumwamba. Angelo a Mulungu ankatsika ndi kumakwera pa makwererowo. Chauta adaimirira pambali pake namuuza kuti, “Ine ndine Chauta, Mulungu wa Abrahamu ndi wa Isaki. Dziko ukugonapoli ndidzakupatsa iwe pamodzi ndi zidzukulu zako. Zidzukulu zakozo zidzachuluka ngati fumbi la pa dziko lapansi. Zidzabalalikira ku mbali zonse: kuzambwe, kuvuma, kumpoto ndi kumwera. Ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadalitsidwa kudzera mwa iwe ndi zidzukulu zako. Ndili nawe, ndidzakutchinjiriza kulikonse kumene udzapite, ndipo ndidzakubwezanso ku dziko lino. Sindidzakusiya mpaka nditachita zonse ndakuuzazi.” Yakobe atadzuka adati, “Ndithudi Chauta ali pano, ndipo ine sindimadziŵa.” Tsono adachita mantha, nanena kuti, “Hi, malo ano ndi oopsa! Zoonadi pano mpa nyumba ya Mulungu ndiponso khomo la kumwamba.” Yakobeyo adadzuka m'maŵa kwambiri, natenga mwala uja adaatsamirawu, nauimiritsa kuti ukhale mwala wachikumbutso. Tsono adauthira mafuta mwalawo. Ndipo malowo adaŵatchula Betele. Poyamba mudziwo unkatchedwa Luzi. Pomwepo Yakobe adalumbira kwa Mulungu, adati, “Mukakhala nane ndi kunditchinjiriza pa ulendo wangawu, ndipo mukandipatsa chakudya ndi zovala, ndi kundibwezera bwino kwathu kwa atate anga, mudzakhala Mulungu wanga. Mwala wachikumbutso ndauimiritsawu udzakhala nyumba yanu, ndipo ine ndidzakupatsani gawo lachikhumi la zonse zimene mudzandipatse.” Tsono Yakobe adapitirira ulendo wake, kupita ku dziko la anthu akuvuma. Atafikako adaona chitsime ku busa, ndiponso magulu atatu a nkhosa zitagona pambali pa chitsimecho. Nkhosazo zinkamwa m'chitsime chimenechi chomwe pamwamba pake panali mwala waukulu. Nkhosa zonsezo zitasonkhana pamodzi kumeneko, abusa oŵeta nkhosazo ndiwo ankachotsa mwalawo pachitsimepo, kuti nkhosa zaozo zimwe. Zitatha kumwako, ankakunkhunizanso mwalawo kutseka pachitsimepo. Yakobe adaŵafunsa abusawo kuti, “Kodi abale anga mukuchokera kuti?” Iwowo adayankha kuti, “Tikuchokera ku Harani.” Yakobe adafunsanso kuti, “Kodi Labani mwana wa Nahori mumamdziŵa?” Iwowo adayankha kuti, “Ee, timamdziŵa.” Adaŵafunsanso kuti, “Kodi ali bwino?” Iwowo adayankha kuti, “Ee, ali bwino. Suuyu Rakele, mwana wake, akubwera ndi nkhosayu.” Tsono Yakobe adati, “Popeza kuti kukali masana, ndipo nthaŵi yokazilonga sinakwane, bwanji osati muzimwetse madzi, muzitengenso kukazidyetsa?” Iwo aja adayankha kuti, “Sitingathe kutero mpaka nkhosa zonse zitasonkhana pamodzi, ndipo mwala wa pamwamba pa chitsimewo titaukunkhuniza. Apo tingathe kuzipatsa madzi nkhosazo.” Yakobe akulankhulabe ndi iwowo, Rakele adafika ndi nkhosa za atate ake. Iyeyo ndiye ankaŵeta nkhosazo. Yakobe ataona Rakele ali ndi nkhosa za bambo wake Labani, adapita kuchitsimeko, nakunkhuniza mwalawo, nkuzimwetsa madzi nkhosa za Labanizo. Tsono Yakobe adamumpsompsona Rakeleyo, nalira mokweza. Ndipo adamuuza kuti, “Ine ndine mwana wa Rebeka, mlongo wa atate ako.” Pomwepo Rakele adathamanga kukauza atate ake. Labani atamva za Yakobe mwana wa mlongo wake, adathamanga kukakumana naye. Adamkumbatira, namumpsompsona, nkupita naye kunyumba. Tsono Yakobe adafotokozera Labani zonse zimene zidachitika. Apo Labani adamuuza kuti, “Inde, zoonadi, iwe ndiwe mbale wanga weniweni.” Yakobe adakhala kumeneko mwezi wathunthu. Tsono Labani adauza Yakobe kuti, “Suyenera kundigwirira ntchito popanda malipiro, chifukwa choti ndife abale. Undiwuze zimene ukufuna kuti ndikulipire.” Labani anali ndi ana aakazi aŵiri, wamkulu Leya, wamng'ono Rakele. Leya anali ndi maso ofooka, koma Rakele anali chiphadzuŵa. Yakobe ankakonda Rakele, ndipo adati, “Ndidzakugwirirani ntchito zaka zisanu ndi ziŵiri chifukwa cha mwana wanu Rakele.” Choncho Labani adati, “Ndi bwino kwambiri kuti Rakeleyu ndipatse iwe, osati munthu wina aliyense. Khala ndi ine.” Motero Yakobe adagwira ntchito zaka zisanu ndi ziŵiri kuti akwatire Rakele, ndipo nthaŵi imeneyo idangooneka kwa iye ngati masiku oŵerengeka chabe, chifukwa choti adaamkonda kwambiri mkaziyo. Yakobe adauza Labani kuti, “Tsopano nthaŵi yatha. Patseni mwana wanuyu kuti ndimkwatire.” Motero Labani adakonza phwando laukwati, naitana anthu onse akumeneko. Koma usiku umenewo Labani adatenga Leya m'malo mwa Rakele nampatsa Yakobe, ndipo Yakobe adaloŵana ndi Leya. (Nthaŵi yomweyo Labani adaperekanso mdzakazi wake Zilipa kwa Leya.) M'maŵa mwake kutacha, Yakobe adaona kuti mkaziyo ndi Leya. Tsono adafunsa Labani kuti, “Chifukwa chiyani mwandichita zotere? Kodi suja ndidakugwirirani ntchito kuti ndikwatire Rakele? Chifukwa chiyani tsono mwandinyenga?” Labani adayankha kuti, “Si mwambo wathu kuno kukwatitsa wamng'ono, mkulu wake asanakwatiwe. Dikira, yamba watsiriza mlungu uno wa chikondwerero chaukwati, kenaka ndidzakupatsa Rakele, komatu udzandigwiriranso ntchito zaka zina zisanu ndi ziŵiri.” Yakobe adavomera, ndipo mlungu wa chikondwerero chaukwati utapita, Labani adapereka Rakele kwa Yakobe kuti akhale mkazi wake. (Nthaŵi yomweyo Labani adaperekanso mdzakazi wake Biliha kwa Rakele.) Motero Yakobe adaloŵana ndi Rakele, ndipo adamkonda kupambana Leya. Tsono adamgwiriranso ntchito Labani zaka zina zisanu ndi ziŵiri. Chauta ataona kuti Yakobe sankakonda kwambiri Leya, adalola kuti Leyayo abale ana, koma Rakele ai. Leya adatenga pathupi, ndipo adabala mwana wamwamuna. Tsono adati, “Chauta waona zovuta zanga. Ndithu tsopano mwamuna wanga adzayamba kundikonda.” Motero mwanayo adamutcha Rubeni. Adatenganso pena pathupi, nabala mwana wina wamwamuna, ndipo adati, “Chauta wandipatsanso mwana wamwamunayu, chifukwa choti adamva kuti mwamuna wanga ine sandikonda.” Motero mwanayo adamutcha Simeoni. Adatenganso pena pathupi, nabalanso mwana wina wamwamuna, ndipo adati, “Tsopano mwamuna wanga azindikonda kwambiri, popeza kuti ndamubalira ana aamuna atatu.” Motero mwanayo adamutcha Levi. Adatenganso pena pathupi, nabala mwana winanso wamwamuna, ndipo adati, “Tsopano ndidzatamanda Chauta.” Motero mwanayo adamutcha Yuda. Apo adayamba walekeza kubala. Rakele ataona kuti sakumubalira ana Yakobe, adayamba kuchita nsanje ndi mkulu wake uja, ndipo adauza Yakobe kuti, “Mundipatse ana, apo ai, ndingofa basi.” Yakobe adapsera mtima Rakele, namuuza kuti, “Sindingathe kuloŵa m'malo mwa Mulungu. Iyeyo ndiye akukuletsa kubala ana.” Apo Rakele adati, “Nayu mdzakazi wanga Biliha, khala nayeni kuti andibalire mwana. Motere podzera mwa iye, inenso ndidzakhala ndi ana.” Choncho Rakele adapereka Biliha kwa mwamuna wake, ndipo adakhala naye. Biliha adatenga pathupi namubalira Yakobe mwana wamwamuna. Tsono Rakele adati, “Mulungu waweruza mondikomera mtima. Wamva pemphero langa, ndipo wandipatsa mwana wamwamuna.” Motero mwanayo adamutcha Dani. Biliha mdzakazi wa Rakele adatenganso pathupi namubaliranso Yakobe mwana wamwamuna. Pamenepo Rakele adati, “Ndalimbana naye kwambiri mkulu wanga, ndipo ndapambana.” Motero mwanayo adamutcha Nafutali. Leya ataona kuti waleka kubala, adapereka mdzakazi wake Zilipa kwa Yakobe. Ndipo Zilipa adabala mwana wamwamuna. Tsono Leya adati, “Ndachita mwai.” Motero mwanayo adamutcha Gadi. Zilipa mdzakazi wa Leyayo adamubaliranso Yakobe mwana wamwamuna wachiŵiri. Apo Leya adati, “Ndakondwa! Ndipo akazi adzanditchula wamwai.” Motero mwanayo adamutcha Asere. Pa nthaŵi yodula tirigu, Rubeni adapita ku minda, nakapezako zipatso za mankhwala a chisulo, ndipo adadzapatsa Leya mai wake. Rakele adauza Leya kuti, “Chonde patseko mankhwala amene mwana wako wakufuniraŵa.” Leya adayankha kuti, “Kodi sunakhutitsidwebe ndi mwamuna wanga udandilandayu? Tsopano ufuna kutenganso mankhwala a chisulo amene mwana wanga wandifunira?” Rakele adati, “Ukandipatsa mankhwala a chisulo ochokera kwa mwana wakoŵa, ŵamunaŵa akhala ndi iwe usiku uno.” Pamenepo Yakobe ankabwera madzulo kuchokera ku munda, Leya adatuluka kukamlonjera, nati “Lero mugone kunyumba kwanga kuno, chifukwa cha mankhwala a chisulo ondifunira mwana wanga.” Motero Yakobe adakhala ndi Leya usiku umenewo. Mulungu adamva pemphero la Leya, choncho adatenga pathupi, namubalira Yakobe mwana wamwamuna wachisanu. Tsono adati, “Mulungu wandipatsa mphotho chifukwa ndidapereka mdzakazi wanga kwa mwamuna wanga.” Motero mwanayo adamutcha Isakara. Leya adatenganso pena pathupi, namubalira Yakobe mwana wamwamuna wachisanu ndi chimodzi. Ndipo adati, “Mulungu wandipatsa mphotho yokoma. Tsopano mwamuna wanga adzakhala nane chifukwa ndamubalira ana aamuna asanu ndi mmodzi.” Motero mwanayo adamutcha Zebuloni. Pambuyo pake adabala mwana wamkazi, namutcha Dina. Tsono Mulungu adakumbukira Rakele, namva pemphero lake, nkulola kuti abale ana. Iyenso adatenga pathupi, nabala mwana wamwamuna. Ndipo adati, “Mulungu wandichotsa manyazi a uchumba wanga.” Motero mwanayo adamutcha Yosefe, nanena kuti, “Mulungu andipatse wina mwana.” Atabadwa Yosefe, Yakobe adauza Labani kuti, “Mundilole ndizibwerera kwathu. Patseni akazi anga ndakugwirirani ntchitoŵa, pamodzi ndi ana anga, ndipo ndichoke. Mukudziŵa kuti ndakugwirirani bwino ntchito.” Labani adamuuza kuti, “Undilole kuti ndinenepo mau aŵa, ‘Ine ndi nzeru zamtundu ndadziŵadi kuti Chauta wandidalitsa chifukwa cha iwe. Tandiwuza malipiro ako, ndikupatsa.’ ” Yakobe adayankha kuti, “Mukudziŵa m'mene ndakugwirirani ntchito, ndi m'mene zoŵeta zanu zaswanirana kwambiri pozisamala ine. Kale munali ndi zoŵeta pang'ono koma tsopano zachuluka, ndipo Chauta wakudalitsani chifukwa cha ine. Tsopano ndiyenera kusamala banja langa.” Apo Labani adamufunsa kuti, “Kodi ndikulipire chiyani?” Yakobe adayankha kuti, “Sindifuna malipiro ena aliwonse. Komabe ndidzapitirira kukuŵeterani zoŵeta zanu, mukavomera kuchita zimene ndinene. Lero ndipita pakati pa zoŵeta zanu zonse. Ndipatula nkhosa zonse zakuda, ndiponso mbuzi zonse zamaŵangamaŵanga ndi zamathothomathotho. Malipiro amene ndifuna ine ndi ameneŵa. Patsogolo pake mudzazindikira ngati ndachita zimenezi mokhulupirika pamene mubwere kudzaona malipiro anga. Mukadzaona kuti ndili ndi mbuzi yopanda mathotho kapena maŵanga kapena mwanawankhosa amene sali wakuda, mudzadziŵe kuti imeneyo ndi yakuba.” Labani adavomera, adati, “Chabwino. Tichite monga waneneramo.” Koma tsiku limenelo, Labani adachotsa atonde onse amathothomathotho ndi amaŵangamaŵanga, kudzanso mbuzi zazikazi zamathothomathotho ndi zamaŵangamaŵanga, zonse za maŵanga oyera. Adachotsanso nkhosa zonse zakuda, nauza ana ake kuti aziyang'anire zoŵeta zonsezo. Atatero adasiyana naye Yakobe uja nayenda mtunda wa masiku atatu. M'menemo nkuti Yakobeyo akuŵeta zoŵeta zina za Labani. Tsono Yakobe adatenga nthambi zaziŵisi za mitengo ya mitundu itatu yakudzikolo, nazikungunula makungwa, kotero kuti nthambizo zinkaoneka za mipyololo yoyera. Nthambizo adaziika patsogolo pa zoŵeta kumene zinkamwera madzi, kuti zoŵetazo ziziyang'ana nthambizo pomwa madzi, chifukwa zoŵetazo zinkakwerewa podzamwa madzi. Motero zoŵetazo zikatenga maŵere zitayang'ana nthambizo, ana ake ankakhala ndi maonekedwe amathothomathotho ndiponso amaŵangamaŵanga. Yakobe adaika anaankhosa padera, naika nkhosa zina kuti ziyang'anane ndi zoŵeta za Labani zamathothomathotho ndi zakuda. Mwa njira imeneyi adapeza zoŵeta zakezake, ndipo sadazisokoneze ndi zoŵeta za Labani. Zoŵeta zamphamvu zikamakwerewa, Yakobe ankazikhazikira nthambi zija kumaso kwake pa malo omwera, kuti pakutero zitenge maŵere pafupi ndi nthambizo. Choncho zoŵeta zikakhala zofooka zinali za Labani, koma zamphamvu zinali za Yakobe. Mwa njira imeneyi Yakobe adalemera kwambiri. Adakhala ndi zoŵeta zambiri, akapolo aamuna ndi aakazi, ngamira ndi abulu. Yakobe adamva kuti ana a Labani ankanena kuti, “Yakobe watenga zonse za bambo wathu. Wapeza chuma chake m'chuma cha bambo wathu.” Yakobe adazindikiranso kuti Labani sankamuwonetsa nkhope yabwino ngati kale. Tsono Chauta adamuuza kuti, “Bwerera ku dziko la atate ako ndi kwa abale ako. Ine ndidzakhala nawe.” Tsono Yakobe adatumiza mau kwa Rakele ndi kwa Leya kuti akakumane naye kubusa kumene kunali zoŵeta zake. Atafikako, iye adaŵauza kuti, “Ndaona kuti bambo wanu tsopano sakundipenya ndi maso abwino ngati kale. Koma Mulungu wa atate anga wakhala nane. Nonse aŵirinu mukudziŵa bwino kuti ndidagwira ntchito kwa bambo wanu ndi mphamvu zanga zonse. Komabe iye wandipusitsa, ndipo malipiro anga waasinthasintha kakhumi konse. Koma Mulungu sadamlole kuti andichite choipa. Nthaŵi zonse Labani akanena kuti, ‘Zoŵeta zamathothomathotho zidzakhala malipiro ako,’ zoŵeta zonse zinkakhala zamathothomathotho. Ndipo akanena kuti, ‘Zamipyololo zikhala malipiro ako,’ zoŵeta zonse zinkangokhala zamipyololo. Mulungu watenga zoŵeta zonse kwa bambo wanu, wapatsa ine. Pa nthaŵi yakuti zoŵeta zitenga maŵere, ine ndidalota maloto, ndipo ndidaona kuti atonde amene ankakwerawo anali amipyololomipyololo, amathothomathotho ndi amaŵangamaŵanga. Ndipo mngelo wa Mulungu adalankhula nane m'maloto momwemo nandiitana kuti, ‘Yakobe,’ ine ndidayankha kuti, ‘Ee Ambuye!’ Iye adati, ‘Tayang'ana, ndipo upenye kuti atonde onse amene akukweraŵa ndi amipyololomipyololo, amathothomathotho ndi amaŵangamaŵanga. Zimenezi ndachita ndine, popeza kuti ndaona zimene Labani akukuchita. Ine ndine Mulungu amene ndidakuwonekera ku Betele kuja kumene udaimika mwala wachikumbutso ndi kuudzoza mafuta, ndipo kumeneko iwe udalumbira. Konzeka tsopano, uchoke kuno, ubwerere ku dziko lakwanu.’ ” Rakele ndi Leya adayankha kuti, “Palibe chomwe chatitsalira ife kwa bambo wathu choti chikhale choloŵa chathu. Ife bambo wathu akutiyesa alendo. Adatigulitsa, ndipo ndalama zomwe adazipezera pa ifezo, adamwaza zonse. Chuma chonse chimene Mulungu wachotsa kwa bambo wathu, ndi chathu ndi cha ana athu. Chitani zimene Mulungu wakuuzani.” Motero Yakobe adakonzekera kuti achoke, kubwerera kwa bambo wake ku dziko la Kanani. Tsono ana ake onse pamodzi ndi akazi ake omwe adaŵakweza pa ngamira. Ndipo zoŵeta zonse adazitsogoza namazikusa, pamodzi ndi zonse zimene adazipeza ku Mesopotamiya kuja. Labani anali atapita kokameta nkhosa. Ndipo akadali komweko, Rakele adaba timilungu ta m'nyumba mwa Labani, bambo wake. Motero Yakobe adampusitsa Labani Mwaramu uja posamuuza kuti akuchoka. Adatenga zake zonse, nachoka chothaŵa. Adanyamuka, naoloka mtsinje wa Yufurate, nkuyamba ulendo wopita ku dziko lamapiri la Giliyadi. Patapita masiku atatu, Labani adamva kuti Yakobe adathaŵa. Tsono adatenga anthu ake, nkulondola Yakobeyo masiku asanu ndi aŵiri, mpaka adakampezera ku dziko lamapiri la Giliyadi. Labani Mwaramu uja adalota maloto usiku womwewo. Mulungu adadza namuuza kuti, “Usamuwopseze Yakobe mwa njira iliyonse.” Labani adampeza Yakobe atamanga mahema kumapiriko. Nayenso Labaniyo adamanga mahema ake komweko ku dziko lamapiri la Giliyadi. Labani adafunsa Yakobe kuti, “Chifukwa chiyani wandinyenga ndi kutenga ana anga aakazi ngati ogwidwa pa nkhondo? Chifukwa chiyani wandinyenga ndi kundizemba osandiwuza? Ukadandiwuza, bwenzi nditakulola mokondwa, ndipo bwenzi pali kumaimba nyimbo ndi ting'oma ndi azeze. Sudandilole kuti nditsazikane ndi adzukulu anga ndi ana anga. Udachita zopusa. Ndili nazo mphamvu zakukuchita choipa. Koma usiku wapitawu, Mulungu wa atate ako wandiwuza kuti, ‘Usamuwopseze Yakobe mwa njira iliyonse.’ Ndikudziŵa kuti udachoka chifukwa unkafunitsitsa kubwerera kwanu. Koma bwanji wandibera timilungu tanga?” Yakobe adayankha kuti, “Ndinkaopa, chifukwa ndinkaganiza kuti mundilanda ana anuŵa. Koma mukapeza kuti wina aliyense pano ali ndi timilungu tanu, aphedwe ameneyo. Anthu tili nawoŵa akhale mboni pano pamene inu muyang'ane zinthu zanu m'katundu yenseyu. Tsono mukazipeza zanuzo mutenge.” Monsemo nkuti Yakobe ali wosadziŵa kuti Rakele adaaba timilunguto. Labani adakaloŵa m'hema la Yakobe ndi m'hema la Leya ndiponso m'hema la adzakazi aŵiri aja, koma sadatipeze timilungu taketo. Kenaka adakaloŵa m'hema la Rakele. Rakeleyo anali ataibisa milungu ya m'nyumba mwa Labaniyo, ataiika pa chishalo cha pamsana pa ngamira, iyeyo nkukhala pomwepo. Labani adafunafuna m'hema monsemo, koma osaipeza. Rakele adauza bambo wake kuti, “Ngati ndikulephera kuimirira pamaso panu, musandikwiyire bambo, chifukwa sindili bwino malinga nza ife akazife.” Motero Labani adalephera kutipeza timilungu ta m'nyumba mwake tija. Apo Yakobe adapsa mtima kwambiri ndipo adalankhula ndi Labani mokalipa, adati, “Kodi ndakulakwirani chiyani? Kodi ndaphwanya lamulo lotani, kuti mundilondole? Tsono mwafunafuna m'katundu wanga yense, kodi mwapeza chiyani chanu? Chomwe mwapezacho muchiike poyera pano, kuti anthu anu ndi anthu angaŵa achiwone. Ndipo iwowo ndiwo aone wokhoza pakati pa aŵirife. Ndakhala nanu zaka makumi aŵiri tsopano, ndipo nkhosa zanu pamodzi ndi mbuzi zomwe sizidapolozepo ai. Ine sindidadyeko nkhosa za m'khola mwanu. Nkhosa ikajiwa ndi zilombo, ine ndinkalipira nthaŵi zonse, sindinkabwera nayo kwa inu, kuwonetsa kuti sindidalakwe. Munkafuna kuti ndilipire chilichonse chobedwa usiku kapena usana. Nthaŵi zambiri ndinkavutika ndi kutentha masana ndiponso ndi kuzizira usiku. Sindinkatha kuwona tulo. Umu ndi m'mene zidaaliri zinthu pa zaka makumi aŵiri zomwe ndidakhala ndi inu. Ndidakugwirirani ntchito zaka khumi ndi zinai chifukwa cha ana anu aŵiriŵa, ndipo zaka zisanu ndi chimodzi ndidagwirira zoŵeta. Komabe malipiro anga mwakhala mukusintha kakhumi konse. Mulungu wa atate anga, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu amene Isaki ankamuwopa, akadapanda kukhala nane, bwenzi mutandichotsa kale ndili chimanjamanja. Koma Mulungu adaona mavuto anga ndi ntchito za manja anga, ndipo usiku wapitawu Iye wakutsutsani.” Labani adayankha Yakobe kuti, “Ana aakaziŵa ndi anga, ana ao ndi anga, pamodzi ndi zoŵeta zomwezi. Zonse ukuziwonazi nzanga. Koma tsopano ndiŵachitire chiyani ana anga aakaziŵa pamodzi ndi ana aoŵa? Chabwino, tiye tichite chipangano, chikhale mboni pakati pa ine ndi iwe.” Yakobe adaimiritsa mwala. Adauza anthu ake kuti asonkhanitse miyala, aunjike mulu. Ndipo pambali pake pa muluwo adadyerapo chakudya. Tsono muluwo Labani adautcha Yagara-Sahaduta, koma mulu womwewo Yakobe adautcha Galedi. Pambuyo pake Labani adati, “Mulu wamiyalawu udzakhala chikumbutso kwa ine ndi iwe.” Nchifukwa chake malowo adaŵatcha Galedi. Labani adanenanso kuti, “Chauta atiyang'anire ife tonse aŵiri pamene tikulekana. Motero malowo adaŵatcha Mizipa. Labani adapitirira kunena kuti, Ukamakaŵazunza ana angaŵa, kapena ukakakwatira akazi ena, ngakhale palibe wina ali nafe pano, ukumbukire kuti Mulungu ndiye mboni pakati pa ine ndi iwe.” Tsono Labani adauza Yakobe kuti, “Pano pali miyala imene ndaunjika pakati pathu, ndipo pompano pali mwala wachikumbutso. Mulu umenewu pamodzi ndi mwala wachikumbutsowu, zonsezi ndi mboni. Ine sindidzapyola mulu umenewu kuti ndilimbane nawe. Iwenso usadzapyole muluwu kuti ulimbane ndi ine. Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Nahori, Mulungu wa atate ao, ndiye adzatiweruze ife aŵiri.” Motero Yakobe adalumbira m'dzina la Mulungu amene Isaki bambo wake ankamuwopa. Tsono Yakobe adapereka nsembe paphiripo, naitana anthu ake kuti adzadye chakudya. Atamaliza kudyako, adagona paphiri pomwepo. M'maŵa mwake, m'mamaŵa, Labani adampsompsona adzukulu ake aja pamodzi ndi ana ake aakaziwo naŵatsazika, ndipo ataŵadalitsa adachoka namapita kwao. Yakobe adanyamuka ulendo wake, ndipo angelo a Mulungu adakumana naye. Ataŵaona, adati, “Ili ndi gulu la ankhondo a Mulungu.” Motero malowo adaŵatcha Mahanaimu. Tsono Yakobe adatuma amithenga ake kwa Esau mbale wake ku Seiri, ku dziko la Edomu. Adaŵalangiza kuti akauze Esau kuti, “Ine Yakobe mtumiki wanu ndinkakhala kwa Labani, ndipo ndakhalitsako mpaka tsopano lino. Ndili ndi ng'ombe, abulu, nkhosa ndi mbuzi ndiponso akapolo ndi adzakazi. Ndikutumiza mau ameneŵa kwa inu mbuyanga, kuti mundikomere mtima!” Amithengawo atabwerera kwa Yakobe adati, “Tidapita kwa mbale wanu Esau, ndipo akubwera kudzakumana nanu. Ali ndi anthu 400 pamodzi.” Apo Yakobe adachita mantha kwambiri ndi kutaya mtima. Motero anthu amene anali nawo adaŵagaŵa m'magulu aŵiri, pamodzi ndi nkhosa, mbuzi, ng'ombe ndiponso ngamira. Mumtima mwake ankaganiza kuti, “Esau akabwera, ndipo akachita nkhondo ndi gulu loyambali, gulu linalo lingathe kuthaŵa.” Pamenepo Yakobe adayamba kupemphera. Adati, “Mulungu wa kholo langa Abrahamu, Mulungu wa bambo wanga Isaki, mundimve ine! Inu Chauta mudandiwuza kuti, ‘Bwerera ku dziko lako, dziko la abale ako, ndidzasamala kuti zinthu zikuyendere bwino.’ Ine sindiyenera kulandira chifundo ndi chikhulupiriro chonse chimene mwandiwonetsa ine mtumiki wanu. Ndidaoloka Yordani ndilibe nkanthu komwe, koma ndodo yokha, koma tsopano ndabwerera ndi magulu aŵiri aŵa. Ndapota nanu, pulumutseni ku mphamvu za mbale wanga Esau. Ndikuwopa kuti mwina akubwera kudzatithira nkhondo, ndipo tonsefe adzatiwononga pamodzi ndi akazi ndi ana omweŵa. Kumbukirani lonjezo lanu lija lakuti, ‘Ndithu ndidzasamala kuti zinthu zikuyendere bwino, ndipo ndidzakupatsa zidzukulu zambiri zosaŵerengeka. Zidzakhala zochuluka ngati mchenga wa m'mbali mwa nyanja.’ ” Atagona kumeneko, pambuyo pake adasankhula mphatso izi pa chuma chonse chimene anali nacho: mbuzi zazikazi 200 ndi atonde makumi aŵiri, nkhosa zazikazi 200 ndi zamphongo makumi aŵiri, ngamira zamkaka makumi atatu pamodzi ndi ana ake, ng'ombe zazikazi makumi anai, ndi zazimuna khumi, ndi abulu aakazi makumi aŵiri ndi amphongo khumi. Gulu lililonse la zoŵeta adalipatsa mnyamata wosamala, ndipo adaŵauza onsewo kuti, “Inu mutsogoleko, ndipo poyenda ndi magulu a zoŵeta, muzisiya mpata pakati pa gulu lililonse.” Adauza mnyamata woyamba kuti, “Mbale wanga Esau akakumana nawe ndi kukufunsa kuti, ‘Kodi mbuyako ndani? Nanga ukupita kuti? Nanga zoŵeta zili patsogolo pakozi nza yani?’ Iwe ukayankhe kuti, ‘Zimenezi ndi za mtumiki wanu Yakobe, ndipo akuzitumiza kwa inu mbuyake, kuti zikhale mphatso. Yakobe mwiniwake ali m'mbuyo mwathumu.’ ” Tsono adauzanso mnyamata wake wachiŵiri mau omwewo, ndi wachitatu, mpaka onse amene ankayenda motsogoza zoŵeta. Adaŵauza kuti, “Zimenezi ndizo mukauze Esau, mukakumana naye. Muzikati, ‘Ndiponso mtumiki wanu Yakobe ali m'mbuyo mwathumu.’ ” Yakobe ankaganiza kuti, “Ndimtsitsa mtima ndi mphatso zimene ndamtumizirazi, ndipo ndikakumana naye, mwina adzandilandira bwino.” Choncho mphatsozo zidatsogola, ndipo usiku umenewo Yakobe adagona kumahema konkuja. Usiku womwewo Yakobe adadzuka natenga akazi ake aŵiri, ndi adzakazi ake aŵiri aja, pamodzi ndi ana ake khumi ndi mmodzi, naoloka mtsinje wa Yaboki padooko pake. Ataŵaolotsa onse aja, adaolotsanso chuma chake chonse. Iye adangotsala yekha. Tsono kudadza munthu wina amene adalimbana naye mpaka m'matandakucha. Munthuyo ataona kuti sakuphulapo kanthu, adamenya Yakobe m'nyung'unyu, nyung'unyuyo nkuguluka polimbanapo. Apo munthuyo adati, “Taye ndizipita, chifukwa kulikucha.” Koma Yakobe adayankha kuti, “Sindikulola kuti upite mpaka utandidalitsa.” Munthuyo adamufunsa kuti, “Dzina lako ndiwe yani?” Yakobe adayankha kuti, “Dzina langa ndine Yakobe.” Munthu uja adati, “Dzina lako silidzakhalanso Yakobe. Walimbana ndi Mulungu ndi anthu, ndipo wapambana. Motero dzina lako lidzakhala Israele.” Pomwepo Yakobe adati, “Choncho nanunso tandiwuzani dzina lanu.” Koma munthuyo adati, “Chifukwa chiyani ukundifunsa dzina?” Ndipo pompo munthu uja adadalitsa Yakobe. Yakobe adati, “Ndamuwona Mulungu maso ndi maso, ndipo ndili moyobe.” Tsono malowo adaŵatcha Penuwele. Dzuŵa lidamtulukira Yakobe pamene ankachoka ku Penuwele, ndipo ankayenda chotsimphina chifukwa cha nyung'unyu ija. Nchifukwa chake mpaka lero lino zidzukulu zonse za Israele sizidya nyama yapanyung'unyu, chifukwa ndi pa mtsempha wa panyung'unyu pomwe Yakobe adaamenyedwa. Yakobe adaona Esau akubwera ndi anthu ake 400. Motero ana ake aja adaŵagaŵira Leya, Rakele ndi adzakazi aŵiri aja. Adatsogoza adzakaziwo pamodzi ndi ana ao. Leya ndi ana ake ankatsata pambuyo pao, Rakele ndi Yosefe ankadza pambuyo penipeni. Yakobe adatsogola, ndipo adaŵerama mpaka pansi kasanu ndi kaŵiri akuyandikira mbale wake. Koma Esau adathamanga kukakumana naye, namkumbatira, ndi kumlonjera pakumumpsompsona. Onse aŵiriwo ankangolira. Esau atayang'ana, adaona akazi ndi ana omwe aja, ndipo adamufunsa kuti, “Anthu aŵa ali ndi iweŵa nga yani?” Yakobe adayankha kuti, “Aŵa, mbuyanga, ndi ana amene Mulungu adandipatsa mwa chifundo chake.” Tsono adzakazi aja adadza pamodzi ndi ana ao, nagwada pansi. Adabweranso Leya pamodzi ndi ana ake, ndipo wotsirizira anali Rakele. Onsewo adagwada pansi. Esau adati, “Nanga gulu la zoŵeta ndakumana nalo lija ndi lachiyani?” Yakobe adayankha kuti, “Mbuyanga, gulu limene lija ndi lanu, kuti inuyo mundikomere mtima.” Koma Esau adati, “Mbale wanga, zoŵeta zotere ndili nazo zambiri. Uli nazozi zikhale zako.” Yakobe adati, “Ai chonde, ngati mwandikomera mtima, landirani mphatso yanga. Ine ndikamaona nkhope yanu, ndiye ngati ndaona nkhope ya Mulungu, poti mwandilandira chonchi ndi manja aŵiri. Chonde landirani mphatso ndakutengeraniyi. Mulungu adandikomera mtima, ndipo adandipatsa zosoŵa zanga zonse.” Adapitirira kumuumiriza, mpaka Esau adalandira. Ndipo Esau adati, “Tiyeni tinyamuke, tizipita. Ine nditsogolako.” Tsono Yakobe adati, “Mbuyanga, mukudziŵa kuti anaŵa atopa, ndipo ndiyenera kusamalanso nkhosa ndi ng'ombe zimene zili ndi tiana. Ndikazikusa mofulumira kwambiri, ngakhale tsiku limodzi lokha, zifa. Chonde mbuyanga, tsogolaniko, ine ndiziyenda pang'onopang'ono pambuyo pa zoŵeta ndi ana anga, mpaka ndikakupezani ku Seiri.” Apo Esau adati, “Tsono undilole kuti ndikusiyire anthu anga enaŵa.” Koma Yakobe adati, “Iyai mbuyanga, zimenezo sizifunika kwenikweni, ndingofuna kukukondwetsani.” Motero pa tsiku limenelo Esau adanyamuka ulendo kubwerera ku Seiri. Koma Yakobe adapita ku Sukoti, ndipo adamangako nyumba yake, pamodzi ndi makola a zoŵeta zake. Nchifukwa chake malowo adatchedwa Sukoti. Pambuyo pake Yakobe adakafika bwino ku mzinda wa Sekemu m'dziko la Kanani, atabwerera kuchokera ku Mesopotamiya. Adamanga mahema pamalo pena, poyang'anana ndi mzindawo. Malo amenewo adagula kwa zidzukulu za Hamori, bambo wake wa Sekemu, pa mtengo wa ndalama 100 zasiliva. Adamanga guwa pomwepo, nalitcha El-Elohe-Israele, ndiye kuti Mulungu, Mulungu wa Israele. Tsiku lina Dina mwana wa Yakobe wobadwa kwa Leya, adapita kukacheza ndi akazi ena am'dzikomo. Sekemu, mwana wa Hamori Muhivi, amene anali mfumu ya chigawo cha dzikolo, atamuwona namwaliyo, adamgwira nagona naye. Sekemu ankamukondadi Dina, mwana wa Yakobe, ndipo ankamulankhula mau achikondi. Choncho adakauza bambo wake kuti, “Nditengereni namwaliyu kuti akhale mkazi wanga.” Yakobe adaamva kuti Dina mwana wake adamgwiririra, koma popeza kuti ana ake aamuna anali ku busa kuŵeta ng'ombe, sadachitepo kanthu mpaka iwowo atabwera. Hamori, bambo wa Sekemu, adapita kukacheza ndi Yakobe. Pa nthaŵi imeneyo ana ake a Yakobewo anali atangobwerako kubusa kuja. Anawo atamva zimenezo, adapsa mtima kwambiri. Adakwiya koopsa poona kuti Sekemu wachita chinthu choipa kwambiri ndi kuchita chipongwe Aisraele, pogwira Dina, mwana wa Yakobe, nkuchita naye zoipa. Tsono Hamori adaŵauza kuti, “Mwana wanga Sekemu wamkonda mwana wanu. Chonde muloleni kuti amukwatire. Tiyeni tikhale ogwirizana chifukwa cha ukwati umenewu. Ife tidzakwatira ana anu, inunso mudzakwatira ana athu. Mukhale nafe pamodzi m'dziko mwathu mommuno. Mukhazikike kulikonse kumene mungakonde, muzichita malonda mwaufulu, ndipo muzigula malo omangira nyumba monga mufunira.” Pambuyo pake Sekemu adauza atate ake a Dina ndi alongo ake aja kuti, “Mundikomere mtima, ndipo ndidzakupatsani zonse zimene mungafune. Tandiwuzani mphatso imene mufuna, ndipo mutchule mtengo uliwonse wolowolera. Ine ndidzakupatsani zonse zimene mungatchule, malinga mukandilola kumkwatira mkaziyu.” Koma ana a Yakobe adayankha Sekemu ndi bambo wake Hamori moŵanyenga, popeza kuti Sekemu adaamchititsa manyazi Dina mlongo wao. Iwowo adati, “Sikungatheke kuti tilole mlongo wathu kukwatiwa ndi munthu wosaumbalidwa. Chimenechi ndi chinthu chamanyazi kwa ife. Tingathe kuvomera pokhapokha inu mutakhala monga momwe tiliri ifemu, ndiye kuti mutaumbala ana anu onse aamuna. Pamenepo tidzakulolani kuti mukwatire ana athu, ndipo ifenso tidzakwatira ana anu. Tsono tidzakhazikika pakati panu ndi kusanduka fuko limodzi. Koma ngati simuvomereza zimene tikunenazi, zoti muumbalidwe, ife tidzangomtenga mwana wathu wamkaziyu.” Mau ameneŵa adakondweretsa kwambiri Hamori ndi mwana wake Sekemu. Ndipo mnyamatayo adafulumira kuchita zimene zinkafunikazo, chifukwa choti adaamkonda kwambiri mwana wa Yakobeyo. Sekemu anali wotchuka kwambiri m'banja lakwaolo. Tsono Hamori pamodzi ndi mwana wake Sekemu adakachita msonkhano ku chipata cha mzinda wao, nalankhula ndi anthu a m'mudzi mwao kuti, “Anthu aŵa ndi abwenzi athu. Motero tiŵalole kuti akhale m'dziko mwathu muno, kuti azichita malonda mwaufulu. Dzikoli ndi lalikulu ndipo lingathenso kuŵakwanira iwowo. Tiyeni tizikwatirana nawo. Komatu anthu ameneŵa adzavomera kukhala pakati pathu ndi kusakanizana nafe, kuti tikhale mtundu umodzi, pokhapokha ifeyo tikaumbala amuna onse monga amachitira iwowo. Nanga sindiye kuti zoŵeta zao, katundu wao ndi ng'ombe zao zidzakhala zathu? Motero tiyeni tivomere kuti azikhala pakati pathu.” Anthu amumzindamo adavomereza zimene Hamori ndi Sekemu adanena, ndipo amuna onse amumzindamo adaumbalidwa. Patangopita masiku atatu, zilonda za kuumbala kuja zisanapole pa anthu aja, ana aŵiri a Yakobe, Simeoni ndi Levi, alongo ake a Dina, adatenga mikondo yao, nakaloŵa mosadziŵika mumzinda muja, nkukapha amuna onse. Adapha Hamori ndi mwana wake Sekemu. Adamtenga Dina kumchotsa m'nyumba mwa Sekemu, nachokapo. Ana ena a Yakobe adafika pa ophedwa aja nafunkha zonse zamumzindamo, chifukwa choti anali atamgwiririra mlongo wao. Adalanda nkhosa, zoŵeta, pamodzi ndi abulu ao ndi zonse zimene zinali mumzindamo ndiponso za ku minda yao. Adatenga chuma chonse, nagwira akazi onse ndi ana, nkutenganso zonse za m'nyumba mwao. Yakobe adauza Simeoni ndi Levi kuti, “Hi, mwandiputira nkhondo. Dzina langa laipa pakati pa anthu a dziko lino, Akanani ndi Aperizi. Ine ndilibe anthu ambiri, tsono iwoŵa akaitanizana kuti adzandithire nkhondo, ine ndi banja langa lonse, tonse pamodzi tidzaonongeka.” Koma iwowo adati, “Pepani, mlongo wathu sangamusandutse mkazi wachiwerewere ai!” Tsono Mulungu adauza Yakobe kuti, “Nyamuka, pita ku Betele, ukakhale komweko. Ukamangeko guwa la Mulungu amene adakuwonekera pamene unkathaŵa mbale wako Esau.” Motero Yakobe adauza banja lake ndi onse amene anali naye kuti, “Tayani milungu yachilendo imene muli nayo pakati panu. Mudziyeretse, ndipo muvale zovala zaudongo. Tichokako kuno, tipita ku Betele kumene ndikamange guwa la Mulungu amene adandithandiza pa nthaŵi ya mavuto anga. Ndiye ndithu amene wakhala nane kulikonse komwe ndinkapita.” Motero milungu yonse yachilendo imene ana ake anali nayo, adaipereka kwa Yakobe, pamodzinso ndi ndolo zakukhutu zimene ankavala. Zonsezo adazifotsera patsinde pa mtengo wa thundu pafupi ndi Sekemu. Pamene Yakobe ndi ana ake adachoka, anthu onse a mizinda yozungulira adachita mantha, motero sadaŵatsatire. Tsono Yakobe adafika ndi anthu ake ku Luzi (ndiye kuti Betele) m'dziko la Kanani. Adamanga guwa kumeneko, ndipo malowo adaŵatcha Betele, chifukwa kumeneko nkumene Mulungu adadziwulula kwa Yakobe pamene ankathaŵa mbale wake. Debora mlezi wa Rakele, adamwalira komweko, ndipo adaikidwa patsinde pa mtengo wathundu ku Beteleko. Motero malowo adatchedwa Mtengo Wamaliro. Yakobe atabwerako ku Mesopotamiya kuja, Mulungu adamuwonekeranso namudalitsa. Mulungu adati, “Dzina lako ndiwe Yakobe, koma kuyambira tsopano, dzina lako lidzakhala Israele.” Motero adayamba kutchedwa Israele. Pambuyo pake Mulungu adamuuza kuti, “Ine ndine Mulungu, Mphambe. Ubale ana ambiri. Udzakhala ndi zidzukulu zambiri, ndipo zina mwa izo zidzakhala mafumu. Zidzukulu zako zidzachuluka kwambiri, kotero kuti zidzakhala mitundu yambiri ya anthu. Ndidzakupatsa dziko limene ndidapatsa Abrahamu ndi Isaki. Dziko limeneli ndidzapatsanso zidzukulu zako, iwe utafa.” Tsono Mulungu adamsiya Yakobe pa malo omwe ankalankhula nayepo, napita. Yakobe adaimika chimwala chachikumbutso pa malo amenewo. Adapereka chopereka cha chakumwa pamwalapo, nathirapo mafuta. Malo amene Mulungu adalankhula naye, Yakobe adaŵatcha Betele. Tsono onse adachoka ku Betele, koma asanafike ku Efurata, nthaŵi yoti Rakele aone mwana idamukwanira, ndipo kubereka kwake kudamuvuta kwambiri. Zidafika poipa kwambiri, ndipo mzamba adamuuza kuti, “Musaope, ameneyu ndi mwana wina wamwamuna.” Tsono Rakele akumwalira kumene, akupuma mwaŵefuŵefu, kutsirizika, adamutcha mwanayo Benoni, koma bambo wake adamutcha Benjamini. Rakele atamwalira, adaikidwa pambali pa mseu wopita ku Efurata (ndiye kuti Betelehemu.) Ndipo Yakobe adaimika chimwala chachikumbutso pa manda a Rakele. Mwalawo ulipobe pamenepo mpaka lero lino. Yakobe adapitirira nakamanga mahema ake kuseri kwa nsanja ya Edere. Pamene Yakobe ankakhala m'dziko limenelo, Rubeni adaachita zoipa ndi Biliha, mmodzi wa azikazi a bambo wake, Yakobeyo nkuzimva zimenezo. Yakobe anali ndi ana aamuna khumi ndi aŵiri. Ana a Leya anali aŵa: Rubeni, mwana wachisamba wa Yakobe, Simeoni, Levi, Yuda, Isakara ndi Zebuloni. Ana a Rakele anali aŵa: Yosefe ndi Benjamini. Ana a Biliha mdzakazi wa Rakele anali aŵa: Dani ndi Nafutali. Ana a Zilipa mdzakazi wa Leya anali aŵa: Gadi ndi Asere. Ameneŵa ndiwo ana a Yakobe amene adabadwira ku Mesopotamiya. Yakobe adakafika kwa bambo wake Isaki ku Mamure (kumenenso kunkatchedwa ku Kiriyati-Ariba kapena Hebroni), kumene Abrahamu ndi Isaki ankakhala kale. Tsono Isaki adamwalira ali wa zaka 180. Ndipo adafa ndi kuikidwa m'manda, ali nkhalamba zedi. Ana ake, Esau ndi a Yakobe ndiwo adamuika m'manda. Nazi zidzukulu za Esau, amene ankatchedwanso Edomu. Esau adaakwatira akazi Achikanani aŵa: Ada mwana wa Eloni Muhiti, Oholibama mwana wa Ana, mwana wa Zibiyoni Muhivi, ndi Basemati mwana wa Ismaele, mlongo wa Nebayoti. Ada adamubalira Esau Elifazi. Basemati adabala Reuele ndipo Oholibama adabala Yeusi, Yalamu ndi Kora. Ameneŵa ndi ana amene adabereka Esau m'dziko la Kanani. Tsono Esau adatenga akazi ake, ana ake aamuna, ana ake aakazi ndi anthu onse a m'nyumba mwake, pamodzi ndi zoŵeta zake zonse, ndi katundu wake yense amene adampeza ku dziko la Kanani, ndipo adasiyana ndi mbale wake uja Yakobe, napita kukakhala ku dziko lina. Chimene adachokera ndi chakuti dziko limene ankakhalako iye pamodzi ndi Yakobe, silinkaŵakwanira aŵiriwo. Anali ndi zoŵeta zochuluka zedi, mwakuti sikudatheke kuti iwo akhale pa malo amodzi. Motero Esau adakakhala m'dziko lamapiri ku Edomu. Nazi zidzukulu za Esau, kholo la Aedomu, okhala m'dziko lamapiri la Seiri. Maina a ana aamuna a Esau naŵa: Elifazi mwana wa Ada mkazi wa Esau, ndi Reuele mwana wa Basemati mkazi wa Esau. Ana a Elifazi ndi Temani, Omara, Zefo, Gatamu ndi Kenazi. (Timna anali mzikazi wa Elifazi mwana wa Esau, ndipo mwa Timnayo Elifazi adaberekamo Amaleke.) Ameneŵa ndiwo ana a Ada mkazi wa Esau. Ana a Reuele ndi aŵa: Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Ameneŵa ndiwo ana a Basemati mkazi wa Esau. Ana a Oholibama mkazi wa Esau ndi aŵa: Yeusi, Yalamu ndi Kora. Oholibamayo anali mwana wa Ana mwana wa Zibiyoni. Naŵa mafumu a zidzukulu za Esau. Mwa ana a Elifazi, mwana woyamba wa Esau, panali mafumu aŵa: Temani, Omara, Zefo, Kenazi, Gatamu ndi Amaleke. Ameneŵa ndi mafumu mwa ana a Elifazi m'dziko la Edomu. Onseŵa anali ana a Ada. Mwa ana a Reuele, mwana wa Esau, panali mafumu aŵa: Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Ameneŵa ndiwo mafumu mwa ana a Ruwele m'dziko la Edomu, ndiponso ndiwo ana a Basemati mkazi wa Esau. Mwa ana a Oholibama, mkazi wa Esau, panali mafumu aŵa: Yeusi, Yalamu ndi Kora. Ameneŵa ndiwo mafumu amene mkazi wa Esau, Oholibama mwana wa Ana, adabala. Ameneŵa ndi zidzukulu zake za Esau, ndiponso ndiwo mafumu ao. Aŵa ndi ana aamuna a Seiri Muhori, nzika za dzikolo: Lotani, Sobali, Zibiyoni ndi Ana, Disoni, Ezere ndi Disani. Aŵa ndiwo mafumu a Ahori ana a Seiri m'dziko la Edomu. Ana a Lotani anali Hori ndi Hemani, ndipo Timna anali mlongo wa Lotani. Ana a Sobali ndi aŵa: Alivani, Manahati, Ebala, Sefo ndi Onamu. Ana a Zibiyoni ndi aŵa: Aya ndi Ana. (Ameneyu ndiye Ana amene adapeza akasupe otentha m'chipululu, pamene ankadyetsa abulu a Zibiyoni bambo wake.) Ana a Ana ndi aŵa: Disoni mwana wake wamwamuna, ndi Oholibama mwana wake wamkazi, Ana aamuna a Disoni ndi aŵa: Hemudani, Esibani, Itirani ndi Kerani. Ana a Ezere ndi aŵa: Bilihani, Zaavani ndi Akani. Ana a Disani ndi aŵa: Uzi ndi Arani. Mafumu a Ahori ndi aŵa: Lotani, Sobali, Zibiyoni, Ana, Disoni, Ezere ndi Disani. Ameneŵa ndiwo mafumu a Ahori m'dziko la Seiri malinga ndi mafuko ao. Naŵa mafumu amene ankalamulira dziko la Edomu, mafumu a Aisraele asanayambe kulamulira kumeneko: Bela mwana wa Beori, ankalamulira dziko la Edomu, ndipo dzina la mzinda wake linali Dinihaba. Bela atafa, Yobabu mwana wa Zera wa ku Bozira ndiye amene adaloŵa ufumu m'malo mwake. Yobabu atafa, Husamu wa ku dziko la Atemani adaloŵa ufumu m'malo mwake. Atafa Husamu, Hadadi mwana wa Bedadi adaloŵa ufumu m'malo mwake. Iyeyu ndiye amene adagonjetsa Amidiyani m'dziko la Mowabu, ndipo dzina la mzinda wake linali Aviti. Atafa Hadadi, Samila wa ku Masireka ndiye adaloŵa ufumu m'malo mwake. Atafa Samila, Shaulo wa ku Rehoboti, mzinda wa pa mtsinje wa Yufurate, ndiye amene adaloŵa ufumu m'malo mwake. Atafa Shaulo, Baala-Hanani mwana wa Akibori, ndiye adaloŵa ufumu m'malo mwake. Baala-Hanani mwana wa Akibori atafa, Hadari ndiye adaloŵa ufumu m'malo mwake. Dzina la mzinda wake linali Pau, ndipo dzina la mkazi wake linali Mehetabele, mwana wa Matiredi mwana wa Mezahabu. Aŵa ndiwo mafumu a kubanja kwa Esau mwatsatanetsatane, malinga ndi mafuko ao ndi malo a fuko lililonse: Timna, Aliva, Yeteti, Oholibama, Ela, Pinoni, Kenazi, Temani Mibizara, Magadiele ndi Iramu. Ameneŵa ndiwo mafumu a Edomu (ndiye kuti Esau kholo la Aedomu potsatana ndi malo omwe ankakhala m'dziko laolo.) Yakobe adakhalabe ku dziko la Kanani kumene bambo wake ankakhala. Mbiri ya banja la Yakobe ndi iyi: Pamene Yosefe anali mnyamata wa zaka 17, ankaŵeta nkhosa ndi mbuzi pamodzi ndi abale ake, ana a Biliha aja ndi a Zilipa, akazi aang'ono a bambo wake. Tsono Yosefeyo ankauza bambo wake zoipa zimene ankachita abale akewo. Israele ankakonda Yosefe kupambana ana ake ena onse, popeza kuti anali mwana wake wapaukalamba. Adamsokera mkanjo wautali wamanja. Abale ake ataona kuti bambo wao ankakonda Yosefe kupambana iwowo, adayamba kudana naye Yosefeyo, ndipo sankalankhula naye mokondwa. Tsiku lina Yosefe adalota maloto, nafotokozera abale ake malotowo. Zitatero, adadana naye kopambana kale. Iye adaŵauza kuti “Mverani maloto omwe ndalota. Tonsefe tinali m'munda, ndipo tinalikumanga mitolo yatirigu. Tilikumanga chomwecho, mtolo wanga unaimirira. Tsono mitolo yanu inauzungulira mtolo wangawo ndi kumauŵeramira.” Apo abale akewo adamufunsa kuti, “Kodi ukuganiza kuti udzakhala mfumu yathu? Kodi ndiye kuti iweyo nkudzatilamula ife?” Motero adadana naye koposa kale chifukwa cha malotowo ndi mau akewo. Tsono Yosefe adalotanso ena maloto, nauzanso abale akewo kuti, “Ndalotanso, ndipo ndaona dzuŵa, mwezi ndi nyenyezi khumi ndi imodzi zikundiŵeramira.” Maloto ameneŵa adauzanso bambo wake pamodzi ndi abale ake omwe aja. Atate ake adamdzudzula, adati, “Kodi maloto ameneŵa ngotani? Kodi ukuganiza kuti ine, mai wakoyu pamodzi ndi abale akoŵa, tidzakugwadira iwe?” Tsono abale ake aja adachita naye kaduka kwambiri. Koma atate ake ankakhala akuziganiza zimenezi. Tsiku lina abale ake a Yosefe adapita ku Sekemu kukaŵeta nkhosa za bambo wao. Israele adauza Yosefe kuti, “Abale ako akuŵeta nkhosa ku Sekemu. Ndikufuna kuti upite kwa iwowo.” Yosefe adayankha kuti, “Chabwino, atate.” Tsono bambo wakeyo adamuuza kuti, “Pita ukaŵaone abale ako m'mene aliri, ndiponso ngati zoŵeta zili bwino, kenaka udzandiwuze.” Choncho bambo wake adatuma Yosefe kuchokera ku chigwa cha Hebroni. Yosefe atafika ku Sekemu, munthu wina adampeza akungoyendayenda m'deralo namufunsa kuti, “Kodi ukufunafuna chiyani?” Yosefe adayankha kuti, “Ndikufunafuna abale anga. Chonde tandiwuzani kumene akuŵeta nkhosa.” Munthuyo adati, “Adachoka kale kuno. Ndidaŵamva akunena kuti akupita ku Dotani.” Apo Yosefe adaŵalondola abale akewo, nakaŵapeza ku Dotani. Abale ake aja adamuwonera kutali, iye asanayandikire nkomwe pamene panali iwopo. Adayamba kumpangira chiwembu natsimikiza zoti amuphe. Onsewo ankauzana kuti, “Uyotu kamaloto uja, akudza apoyo! Tiyeni timuphe, mtembo wake tiwuponye m'chitsime china mwa zitsime zili apazi. Tizikanena kuti wajiwa ndi chilombo, ndipo tidzaone tanthauzo lake la maloto ake aja.” Tsono Rubeni adamva zimene enawo ankanena, ndipo adayesetsa kumpulumutsa Yosefe. Adati, “Ai tisamuphe, tisakhetse magazi ake. Tingomuponya m'chitsime chopanda madzichi kuchipululu konkuno. Tisampweteke konse.” Ankanena zimenezi akuganiza zomupulumutsa m'manja mwao, kuti amtumize kwa bambo wake. Yosefe atafika kumene kunali abale akewo, iwowo adamuvula mkanjo wake, uja wautali wamanjawu umene adaavala, namtenga, nkumuponya m'chitsime chopanda madzi. Pamene iwo ankadya, adaona gulu la Aismaele akuchokera ku Giliyadi. Ngamira zao zinali zitasenza nzonono ndi zonunkhira zimene ankapita nazo ku Ejipito. Tsono Yuda adafunsa abale ake kuti, “Kodi tipindulanji tikamupha mbale wathuyu ndi kubisa, osaulula kuti tamupha? Tiyeni timgulitse kwa Aismaeleŵa. Nanga iyeyu si mbale wathu, thupi limodzi ndiponso magazi amodzi?” Abale akewo adavomereza zimenezo. Tsono Amidiyani ena amalonda adafika pomwepo. Abale akewo adamtulutsa Yosefeyo m'chitsime muja, namgulitsa kwa Aismaelewo pamtengo wokwana masekeli a siliva makumi aŵiri, ndipo iwowo adapita naye ku Ejipito. Rubeni atabwerera kuchitsime kuja, adapeza muli ng'waa! Pomwepo adang'amba zovala zake chifukwa cha chisoni. Ndipo adabwerera kwa abale ake aja naŵauza kuti, “Mnyamata ujatu palibe! Tsono ine ndichite chiyani?” Pomwepo iwo adapha mbuzi, naviika mkanjo wa Yosefe uja m'magazi ake. Adatenga mkanjowo napita nawo kwa bambo wao, nati, “Tayang'anani, kapena nkukhala mkanjo wa mwana wanu uja.” Yakobe adauzindikira mkanjowo, nati, “Ha, ndi wakedi! Chilombo chamupha mwana wanga. Kalanga ine, Yosefe wakadzulidwa!” Yakobe adang'amba zovala zake, navala chiguduli m'chiwuno, chifukwa cha chisoni. Adalira maliro a mwana wakeyo nthaŵi yaitali. Ana ake onse aamuna ndi aakazi, adabwera kuti amtonthoze koma iye adakana, adati, “Ndidzakhala ndikulira mwana wanga mpaka kumanda komwe kuli iyeko.” Choncho adapitirirabe kulira chifukwa cha Yosefe mwana wake. Nthaŵi imeneyo nkuti Amidiyani aja atamgulitsa Yosefe kwa Potifara ku Ejipito. Potifarayo anali mmodzi mwa nduna za Farao, ndipo anali mkulu wa asilikali olonda kunyumba kwa Farao. Nthaŵi imeneyo Yuda adachoka nakakhala kwa munthu wina wa fuko la Adulamu dzina lake Hira. Kumeneko Yuda adaonako mtsikana Wachikanani, mwana wa Suwa, namkwatira. Mkaziyo adatenga pathupi nabala mwana wamwamuna, nkumutcha Ere. Adatenganso pena pathupi nabala mwana wamwamuna, nkumutcha Onani. Adabalanso mwana wina wamwamuna, namutcha Sela. Pamene Sela ankabadwa, nkuti Yuda ali ku Kezibu. Yuda adampezera mkazi mwana wake wachisamba uja Ere, dzina lake Tamara. Koma makhalidwe oipa a Ere adaipira Chauta, mwakuti Chauta adamlanga ndi imfa. Motero Yuda adauza Onani kuti, “Loŵana naye mkazi wamasiye wa mbale wakoyu. Uloŵe chokolo ndithu, kuti mbale wakoyo akhale ndi ana.” Koma Onani adaadziŵa kuti anawo sadzakhala ake. Motero nthaŵi zonse akamakhala naye mkaziyo, ankangotayira pansi mbeu yake, kuti asamubalire ana mbale wakeyo. Tsono zimene ankachitazo zidaipira Chauta ndipo Chauta adamlanganso ndi imfa. Apo Yuda adauza mpongozi wake uja Tamara kuti, “Bwererani kunyumba kwa bambo wanu, mukakhale wamasiye kumeneko mpaka mwana wanga Sela atakula.” Adanena zimenezi chifukwa ankaopa kuti Sela angafenso monga abale akewo. Motero Tamara adabwerera kunyumba kwa bambo wake. Patapita nthaŵi, mkazi wa Yuda uja, mwana wa Suwa, adamwalira. Tsono Yuda atatha kulira malirowo, iyeyo pamodzi ndi bwenzi lake Hira Mwadulamu, adapita ku Timna kumene ankameta nkhosa zake. Munthu wina adauza Tamara kuti, “Apongozi ako akupita ku Timna kukameta nkhosa.” Tsono Tamarayo adasintha zovala zake zaumasiye zija navala zina. Adadziphimba kumaso ndi nsalu, nakakhala pansi pa chipata cha ku Enaimu. Mudzi wa Enaimu unali pa mseu wopita ku Timna. Adaadziŵa kuti pa nthaŵiyo nkuti Sela atakula, komabe Tamara anali asanamloŵe chokolo Sela uja. Yuda atamuwona, adaamuyesa mkazi wadama, chifukwa anali atadziphimba kumaso. Adapita ku mbali ya mseu komwe kunali iyeyo namuuza kuti, “Kodi mungandilole kuti ndigone nanu?” Yuda sankadziŵa kuti ndi mpongozi wake. Mkaziyo adati, “Mudzandipatsa chiyani?” Yuda adayankha kuti, “Ndidzakutumizira mbuzi yaing'ono ya m'khola mwanga.” Tsono Tamarayo adati, “Chabwino, ndivomera mukandipatsa chikole choti mpaka mudzanditumizire.” Yuda adamufunsa kuti, “Kodi ukufuna chikole chotani?” Tamara adayankha kuti, “Mundipatse mphete yanu pamodzi ndi chingwe chanu chomwecho, ndi ndodo yanu yoyendera imene ili m'manja mwanuyi.” Yuda adapereka zonsezo kwa Tamara. Atatero Yuda adagona naye mkaziyo, ndipo adatenga pathupi. Tsono Tamara adanyamuka nachokapo. Adachotsa nsalu imene adaadziphimba nayo kumaso ija, navalanso zovala zake zaumasiye zija. Pambuyo pake Yuda adatuma bwenzi lake kukapereka mbuzi ija, kuti mkazi uja amubwezere zikole zija. Koma bwenzi lakeyo sadakampeze mkaziyo. Adafunsa anthu akomweko kuti, “Kodi mkazi wadama amene ankakhala pambali pa mseu wopita ku Enaimu uja ali kuti?” Anthuwo adayankha kuti, “Chikhalire sipadakhale mkazi wadama pa malo amenewo.” Adabwerera kwa Yuda nakamuuza kuti, “Sindidampeze mkazi uja, ndipo anthu akumeneko andiwuza kuti, ‘Chikhalire sipadakhale mkazi wadama pa malo amenewo.’ ” Yuda adati, “Zinthu zimenezo atenge zikhale zake, kuwopa kuti anthu angadzatiseke. Ngakhale sudampeze mkaziyo, komabe ine ndidaamtumizira ndithu mbuziyi.” Patapita miyezi itatu, munthu wina adauza Yuda kuti, “Mpongozi wanu uja Tamara adachita chigololo, ndipo ali ndi pathupi.” Pomwepo Yuda adalamula kuti, “Kamtengeni ndipo mukamtenthe kuti afe.” Akutengedwa kumene, Tamarayo adatumiza mau kwa Yuda mpongozi wake kuti, “Ine ndili ndi pathupi pa mwiniwake zinthu izi. Taziyang'anani, muwone mwina inu nkumudziŵa mwiniwakeyo kuti ndani: mpheteyi ndi chingwechi ndiponso ndodo yoyenderayi.” Yuda atazizindikira zinthuzo adati, “Akunenetsadi. Ndine amene ndidalakwa. Bwenzi nditampereka kwa mwana wanga Sela kuti amkwatire.” Choncho Yuda sadagone nayenso mkaziyo. Itakwana nthaŵi yakuti Tamara achire, m'mimba mwake munali mapasa. Pa nthaŵi yochira, mmodzi mwa anawo adatulutsa dzanja. Mzamba adaligwira, nalimanga ndi chingwe chofiira nati, “Ameneyu ndiye woyamba kubadwa.” Koma mwanayo adalibweza dzanja lake, mwakuti mbale wake ndiye adayambira kubadwa. Tsono mzamba uja adati, “Uchita kudziphothyolera wekha chotere!” Motero mwanayo adatchedwa Perezi. Pambuyo pake mbale wake adabadwa chingwe chofiira chija chili lende ku dzanja. Tsono iyeyu adatchedwa Zera. Aismaele aja adapita naye Yosefe ku Ejipito kumene Potifara Mwejipito, nduna ya Farao ndiponso mkulu wa asilikali olonda kunyumba ya mfumu, adamgula. Chauta anali naye Yosefe, ndipo adamthandiza kuti zonse zimuyendere bwino. Adakhala m'nyumba ya bwana wake, Mwejipito uja. Bwana wakeyo adaona kuti Chauta anali naye Yosefe, ndi kuti ankamukhozetsa pa zonse zimene ankachita. Potifara adakondwa naye Yosefe poona m'mene ankamutumikira. Choncho adamsandutsa kapitao wa nyumba yake, ndiponso woyang'anira zonse zam'nyumbamo. Kuyambira nthaŵi imene Yosefe adayamba kusamalira zonse za m'nyumba ya Potifarayo, Chauta adadalitsa zonse za kunyumba kwa Mwejipitoyo, ngakhale za kuminda kwake, chifukwa cha Yosefeyo. Choncho Potifara adaika m'manja mwa Yosefe zake zonse, kotero kuti sankalabadiranso kanthu kalikonse, koma chakudya chokha chimene ankadya. Yosefe anali wa maonekedwe abwino ndi wokongola. Patapita kanthaŵi, mkazi wa bwana wake adayamba kusirira Yosefe. Tsono mkaziyo adauza Yosefeyo kuti, “Bwanji ugone nane.” Yosefe adakana, adati, “Chifukwa choti ine ndikugwira ntchito muno, bwana wanga salabadiranso kanthu kalikonse ka m'nyumba muno. Adandipatsa ukapitao woyang'anira zake zonse, ndipo ulamuliro wa zonse za m'nyumba muno uli m'manja mwanga, osati m'manja mwake. Sadandimane kanthu kalikonse kupatula inu nokha, pakuti ndinu mkazi wake. Tsono kungatheke bwanji kuti ine ndichite chinthu choipitsitsa choterechi, ndi kuchimwira Mulungu?” Ngakhale mkazi uja ankalankhula mau ameneŵa kwa Yosefe tsiku ndi tsiku, Yosefeyo sankamvako mpang'ono pomwe, ndipo sankalola kuchita naye zoipa. Koma tsiku lina Yosefe adaloŵa m'nyumba kuti agwire ntchito, ndipo panalibe antchito ena m'nyumbamo. Mkazi uja adamgwira mwinjiro Yosefeyo, namuuza kuti, “Ugone nane basi!” Koma iye adathaŵira pabwalo, kusiya mwinjiro uja uli m'manja mwa mkaziyo. Tsono mkazi uja ataona kuti Yosefe wasiya mwinjiro ndipo wathaŵira pabwalo, adaitana antchito am'nyumbamo, naŵauza kuti, “Mwaziwona izi? Mwamuna wanga adabwera ndi Muhebri uyu m'nyumba muno kudzatipunza ife. Iye anakaloŵa kuchipinda kwanga nandinyenga kuti ndigone naye. Koma ine ndinakuŵa kwambiri. Tsono atamva kukuwa kwangako, wasiya mwinjiro wake m'manja mwangamu nkuthaŵira pabwalo.” Mwinjirowo adangousunga m'manja kudikira mpaka bwana wa Yosefe atabwera. Tsono atabwera, adamsimbira nkhani yonseyo, adati, “Kapolo uja Wachihebri mudabwera naye m'nyumba munoyu, analoŵa kuchipinda kwanga kukandipunza ine. Koma ine nditakuwa, iyeyo anasiya mwinjiro wake pafupi ndi ine, nkuthaŵira pabwalo.” Mbuyake wa Yosefe adapsa mtima koopsa atamva mau a mkazi wake onena kuti, “Inde, izi ndi zimene wandichita kapolo wanu.” Pompo adammangitsa Yosefe nakamtsekera m'ndende m'mene ankasungamo akaidi a mfumu, ndipo adakhala m'menemo. Koma Chauta anali naye Yosefe, namkomera mtima kwambiri, kotero kuti wosunga ndende adakondwera naye Yosefe. Adamsandutsa kapitao woyang'anira akaidi anzake onse, pamodzi ndi zonse zochitika m'ndendemo. Zonse zinali m'manja mwa Yosefe, ndipo wosunga ndendeyo sankayang'aniranso kanthu kena kalikonse, chifukwa Chauta anali naye Yosefe ndipo ankamukhozetsa pa zonse zimene ankachita. Patapita kanthaŵi, munthu woperekera vinyo pamodzi ndi wopanga buledi ku nyumba ya mfumu ya ku Ejipito, adalakwira mbuyao mfumu. Farao adaŵakwiyira kwambiri antchito ake aŵiriwo. Motero adaŵatsekera m'ndende, nakaŵaika m'manja mwa mkulu wa asilikali olonda kunyumba kwa mfumu uja, m'ndende momwe Yosefe ankasungidwa. Mkulu wa alonda uja adasankhula Yosefe kuti asamalire anthu aŵiriwo ndi kuŵalonda. Adakhalamo nthaŵi yaitali ndithu m'ndendemo. Usiku wina m'ndendemo, anthu aŵiri onse aja, woperekera vinyo uja ndi wophika buledi, adalota maloto. Aliyense mwa aŵiriwo adalota maloto ake a tanthauzo lakelake. Yosefe atabwera m'maŵa, adaona kuti nkhope zao zasinthika. Adaŵafunsa kuti, “Mwatani mukuwoneka ngati achisoni lero?” Onsewo adayankha kuti, “Aŵirife tonse talota maloto usiku wapitawu, ndipo pano palibe ndi mmodzi yemwe wotha kutimasulira malotowo.” Apo Yosefe adaŵauza kuti, “Ndi Mulungu yekhatu amene amapatsa nzeru zomasulira maloto. Tandiwuzani maloto anuwo.” Motero uja woperekera vinyoyu adayambapo kunena maloto ake, adati, “Ine ndinalota ndikuwona mtengo wamphesa, unali ndi nthambi zitatu. Masamba ake atangophukira, pomwepo panaoneka maluŵa, pambuyo pake panaonekanso mphesa zakupsa. Chikho cha Farao chinali m'manja mwanga; ine ndinatenga mphesazo nkufinyira m'chikhomo, ndipo ndinachipereka kwa Farao.” Yosefe adamuyankha kuti, “Tanthauzo lake la maloto ameneŵa nali: nthambi zitatuzo ndi masiku atatu. Pakangopita masiku atatu, Farao akutulutsa muno, akukhululukira, ndipo akubwezera pa ntchito yako. Tsono uzidzaperekera chikho kwa Farao monga momwe unkachitira kale. Komatu udzandikumbuke, zinthu zikadzakuyendera bwino. Chonde udzandikomere mtima ndi kutchula dzina langa kwa Farao, kuti ndidzatulule m'ndende muno. Inetu adachita chondiba, ndipo adabwera nane kuno kuchokera ku dziko la Ahebri. Tsono ngakhale kunoko, sindidachite kanthu kalikonse koti anditsekere nako m'ndende.” Wophika buledi uja nayenso adaona kuti tanthauzo la malotowo linali labwino, adauza Yosefe kuti, “Inenso ndinalota nditasenza nsengwa zitatu za buledi pamutu pangapa. M'nsengwa yapamwamba munali mitundu yambiri ya chakudya cha Farao, koma mbalame zinalikudya chakudyacho.” Yosefe adamuyankha kuti, “Kamasulidwe kake ka maloto ameneŵa ndi aka: nsengwa zitatu ndi masiku atatu. Pakapita masiku atatu, Farao akutulutsa muno, ndipo adzadula mutu wako. Tsono mtembo wako adzaupachika pa mtengo, ndipo mbalame zidzadya mnofu wako.” Patangopitadi masiku atatu, padachitika phwando lokondwerera tsiku lobadwa Farao, ndipo Faraoyo adaitana nduna zake zonse. Tsono adamtulutsa uja woperekera vinyoyu pamodzi ndi wophika buledi yemwe uja. Aŵiri onse aja adaŵaimika pamaso pa nduna zake zija. Farao adamubwezera pa tchito yake woperekera vinyo uja. Koma wophika buledi uja adampachika, monga momwe Yosefe adaanenera pomasulira maloto ao aja. Komabe woperekera vinyo uja sadamkumbuke Yosefe, adangomuiŵaliratu. Patapita zaka ziŵiri, Farao adaalota kuti waimirira pamphepete pa mtsinje wa Nailo. Nthaŵi yomweyo adangoona ng'ombe zisanu ndi ziŵiri zonenepa bwino zikutuluka mumtsinjemo, nkuyamba kudya msipu wam'mabango. Kenaka mumtsinje momwemo mudatulukanso ng'ombe zina zisanu ndi ziŵiri zoonda ndi zofooka, zimene zidaima pa mtunda pafupi ndi ng'ombe zina zija. Tsono ng'ombe zoondazo zidadya zinzake zonenepa zija. Pamenepo Farao adadzuka. Atagonanso, adalota enanso maloto. Adaona ngala zatirigu zisanu ndi ziŵiri zitabala pa mphesi imodzi, ndipo zinali zakucha ndi zokhwima. Kenaka padaphukanso ngala zina zisanu ndi ziŵiri zofwapa ndi zopserera ndi mphepo yamkuntho yakuvuma. Ngala zofwapazo zidameza ngala zisanu ndi ziŵiri zokhwima zija. Farao atadzuka, adaona kuti anali maloto chabe. Kutacha m'maŵa adavutika kwambiri, mwakuti adaitana amatsenga ake onse ndi anthu anzeru onse a ku Ejipito. Onsewo atabwera, Farao adaŵafotokozera maloto akewo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe amene adatha kuŵamasula. Pomwepo woperekera vinyo uja adauza Farao kuti, “Lero ndiwulule kulakwa kwanga. Paja inu mfumu mudaatipsera mtima antchitofe. Ndipo ine ndi wophika buledi tonse mudaatitsekera m'ndende, m'nyumba ya mkulu wa alonda. Tsono usiku wina, aŵirife tidaalota maloto. Aliyense mwa ife anali atalota maloto ake, a tanthauzo lakelake. M'nyumba momwemo munali mnyamata wina Wachihebri, mtumiki wa mkulu wa alonda a m'ndende muja. Iyeyo adammasulira bwino aliyense mwa ife tanthauzo la maloto akewo. Ndipo zidachitikadi monga momwe adaatimasulira. Ine ndidabwerera pa ntchito yanga, koma wophika buledi uja adampachika pa mtengo.” Tsono Farao adaitanitsa Yosefe, ndipo adamtulutsa msanga kundendeko. Iyeyo atameta bwino ndi kusintha zovala, adapita kwa Farao kuja. Farao adauza Yosefe kuti, “Ine ndidalota maloto, koma palibe ndi mmodzi yemwe amene akutha kumasula malotowo. Tsono adandiwuza kuti iwe ukamva maloto, ati umadziŵa kumasula kwake.” Yosefe adayankha kuti, “Sindine ai, koma Mulungu ndiye amene adzatha kuimasulira mfumu maloto ameneŵa.” Apo Farao adati, “Ine ndidaalota ntaimirira pamphepete pa mtsinje wa Nailo. Nthaŵi yomweyo ndidangoona ng'ombe zisanu ndi ziŵiri zonenepa bwino zitatuluka mumtsinjemo, nkuyamba kudya msipu wam'mabango. Kenaka padatulukanso ng'ombe zina zisanu ndi ziŵiri zoonda ndi za maonekedwe oipa kwambiri. Ng'ombe zimenezo zinali zoonda kwambiri kupambana ng'ombe zoonda zonse za m'dziko lonse la Ejipito. Ng'ombe zoondazo zidadya zinzake zonenepa zija. Koma zitadya zinzakezo, palibe ndi mmodzi yemwe akadazindikira, popeza kuti ng'ombe zoondazo sizidasinthike konse kaonekedwe kake, koma zidangokhala zoonda ndithu monga kale. Tsono ndidadzuka. Nditagonanso ndidalota ntaona ngala zatirigu zisanu ndi ziŵiri zakucha ndi zokhwima bwino zitabala pa mphesi imodzi. Pomwepo padaphukanso ngala zina zatirigu zisanu ndi ziŵiri zofwapa, zopserera ndi mphepo yakuvuma. Ngala zofwapazo zidameza zinzake zokhwima zija. Tsono ndidafotokozera amatsenga maloto ameneŵa, koma palibe ndi mmodzi yemwe amene adatha kundimasulira.” Apo Yosefe adauza Farao kuti, “Maloto onse aŵiriŵa ali ndi tanthauzo limodzi lokha. Mulungu wakuuziranitu zimene adzachite. Ng'ombe zisanu ndi ziŵiri zonenepazo ndi zaka zisanu ndi ziŵiri. Ndipo ngala zatirigu zisanu ndi ziŵiri zokhwimazo nazonso ndi zaka zisanu ndi ziŵiri. Kumasula kwake nkumodzi. Ng'ombe zisanu ndi ziŵiri zoonda zimene zidabwera pambuyo zija, ndiponso ngala zatirigu zisanu ndi ziŵiri zopserera ndi mphepo yakuvuma zija, ndi zaka zisanu ndi ziŵiri za njala. Tsono monga momwe ndanenera, ndiye kuti Mulungu wakuuziranitu zomwe adzachite. Padzakhala zaka zisanu ndi ziŵiri za dzinthu dzambiri m'dziko lonse la Ejipito. Zitapita zaka zimenezo, padzakhalanso zaka zisanu ndi ziŵiri za njala, ndipo zaka zonse zija za dzinthu zidzaiŵalika mu Ejipito monse. Njalayo idzaononga dziko. Zaka zonse zija za dzinthu dzambiri sizidzakumbukikanso, chifukwa njala imene idzabwereyo idzakhala yoopsa. Poti inu Farao mwalota kaŵiri maloto okhaokhaŵa, zikuwonetsa kuti Mulungu ndiye amene wakonza zimenezi, ndipo azichitadi posachedwa. Tsopano inu mfumu sankhulani munthu wodziŵa zinthu ndi wanzeru, mumpatse ulamuliro pa dziko lonse la Ejipito. Musankhenso anthu akuluakulu m'dziko lonse lino, ndipo chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse za zokolola, azichiika padera pa zaka zisanu ndi ziŵiri za chakudya chochuluka. Asonkhanitse chakudya chonse cha zaka zadzinthu zimene zikubwerazi. Azichita zonsezi ndi ulamuliro wanu, ndipo aziika tirigu padera m'mizinda yonse ndi kumsunga bwino. Chakudya chimenecho chidzakhala chakudya cha nthaŵi ya njala ya zaka zisanu ndi ziŵiri imene idzabwere ndithu mu Ejipito muno, kuti choncho anthu a ku Ejipito asadzafe ndi njala.” Farao pamodzi ndi nduna zake adavomereza zonse zimene adaanena Yosefe. Tsono Farao adafunsa nduna zakezo kuti, “Kodi tingampeze kuti munthu wina woposa uyu amene ali ndi mzimu wa Mulungu?” Motero Farao adauza Yosefe kuti, “Popeza kuti Mulungu wakuwonetsa zonsezi, palibenso wina aliyense wodziŵa zinthu ndi wanzeru kupambana iweyo. Iwe ndiwe amene udzalamulira dziko langa, ndipo anthu anga onse adzakumvera. Ine ndidzakupambana pa chokhachi choti ndine mfumu.” Tsono Farao adauzanso Yosefe kuti, “Tsopano ine ndakusankhula iweyo kuti ukhale nduna yaikulu ya dziko lonse la Ejipito.” Atatero, Farao adavula mphete yaufumu ku chala chake, naiveka ku chala cha Yosefe. Adamuvekanso zovala zabafuta ndi ukufu wagolide m'khosi mwake. Adamkweza pa galeta lake lachiŵiri laufumu, ndipo alonda ake a Farao adayamba kufuula patsogolo pa galetalo kuti, “Mgwadireni.” Motero Yosefe adalandira ulamuliro, ndipo adakhala nduna yaikulu ya dziko lonse la Ejipito. Farao adauza Yosefe kuti, “Pali ine ndemwe Farao, iwe ukapanda kulola, palibe ndi mmodzi yemwe amene adzathe kuchita kanthu kalikonse ngakhale kuyenda kumene m'dziko la Ejipito lonseli.” Pamenepo Yosefe uja adamutcha Zafenati-Panea. Ndipo adampatsa mkazi dzina lake Asenati, mwana wa Potifera amene anali wansembe wa mzinda wa Oni. Choncho Yosefeyo adayendera dziko lonse la Ejipito. Yosefe anali wa zaka makumi atatu pamene adayamba kugwirira ntchito Farao mfumu ya ku Ejipito. Adanyamuka, nayendera dziko lonse. Pa zaka zija za dzinthu dzambiri, m'dziko lonse munali chakudya chochuluka kwambiri. Yosefe adasonkhanitsa chakudya pa zaka zisanu ndi ziŵiri, pamene kunali dzinthu dzambirimbiri ku Ejipito, nadzisunga m'mizinda. Mu mzinda uliwonse ankasungamo chakudya cha ku minda yozungulira mzindawo. Adasonkhanitsa tirigu wochuluka ngati mchenga wakunyanja. Kunali tirigu wochuluka kotero kuti adaaleka nkumuyesa komwe, popeza kuti kunali kosatheka kumuyesa tirigu yenseyo. Zaka zanjala zisanafike, Yosefe adabereka ana aamuna aŵiri mwa Asenati uja, mwana wa Potifera, wansembe wa ku Oni. Tsono adati, “Mulungu wandiiŵalitsa kusauka kwanga konse kuja ndiponso banja la atate anga.” Motero mwana wake wachisamba uja adamutcha Manase. Ndipo adanenanso kuti, “Mulungu wandipatsa ana m'dziko la masautso anga.” Motero mwana wachiŵiriyo adamutcha Efuremu. Zaka zisanu ndi ziŵiri za dzinthu zitatha, kudafika zaka zisanu ndi ziŵiri za njala zimene ankanena Yosefe zija. Njala imeneyo inali itafikanso ku maiko ena onse, koma m'dziko lonse la Ejipito munali chakudya chambiri. Njalayo itakwanira dziko lonse la Ejipito, anthu ankalirira Farao kuti aŵapatse chakudya. Farao ankaŵauza onse kuti, “Pitani kwa Yosefe, zimene akakulamuleni, mukachite zimenezo.” Tsono njalayo itakwanira dziko lonse, Yosefe adatsekula nkhokwe za tirigu zija, namaŵagulitsa Aejipitowo, chifukwa inali itakula ndithu mu Ejipitomo. Anthu ankafika ku Ejipito kuchokera ku mbali zonse za dziko lapansi, kudzagula tirigu kwa Yosefe, chifukwa njala inali itakula koopsa konsekonse. Yakobe atamva kuti ku Ejipito ndiko kuli tirigu, adafunsa ana ake kuti, “Chifukwa chiyani mukungokhala osachitapo kanthu? Ndikumva kuti ku Ejipito aliko tirigu. Pitaniko kumeneko, mukatigulireko ife, kuti tingafe ndi njala.” Motero abale ake a Yosefe khumi adanyamuka kupita ku Ejipito kukagula tirigu. Yakobe sadamtume nawo Benjamini, mng'ono wake weniweni wa Yosefe uja, chifukwa ankaopa kuti angapeze tsoka. Ana a Israelewo adapita ku Ejipito kukagula chakudya pamodzi ndi anthu ena onse, chifukwa chakuti ku dziko la Kanani kunali njala. Tsono popeza kuti Yosefe anali nduna yaikulu yolamulira dziko lonse la Ejipito, ndiye amene ankagulitsa tirigu kwa anthu ochokera ku mbali zonse za dziko. Choncho abale ake a Yosefe nawonso adabwera, ndipo adamgwadira Yosefeyo, namuŵeramira. Yosefe ataŵaona abale akewo, adaŵazindikira, koma adangochita ngati sadaŵadziŵe. Adayamba kuŵalankhula mozaza, naŵafunsa kuti, “Kodi inu mukuchokera kuti?” Iwo adayankha kuti, “Tikuchokera ku Kanani, tadzagula chakudya kuno.” Yosefe adaŵazindikira abale ake aja, koma iwo sadamzindikire. Adakumbukira maloto aja onena za iwo, ndipo adati, “Ndinu anthu ozonda dziko. Mwabwera kuno kudzazonda kuti muwone ngati dziko lathu ndi lofooka.” Iwo aja adayankha kuti, “Iyai mbuyathu, ife atumiki anu tabwera kuti tidzagule chakudya basi. Tonsefe tili pachibale. Sindife azondi, mbuyathu, koma ndife anthu okhulupirika ndithu.” Yosefe adati, “Iyai. Inu mwabwera kudzazonda dziko lathu kuti muwone ngati ndi lofooka.” Tsono iwowo adati, “Mbuyathu, ife tinalipo ana aamuna khumi ndi aŵiri pachibale pathu, bambo wathu mmodzi, ku dziko la kwathu ku Kanani. Wamng'ono ali ndi bambo wathu, ndipo wina adamwalira.” Koma Yosefe adaŵayankha kuti, “Paja ndanena kale kuti ndinu azondi basi. Tsono ndikuyesani motere; ndikulumbira kuti pali Farao! Inuyo simuchoka, mpaka mng'ono wanuyo atabwera kuno. Tumani mmodzi mwa inu kuti apite akamtenge. Ena nonse otsalanu mukhale m'ndende ndithu, mpaka mau anuŵa atsimikizike, tiwone ngati mukunena zoona. Apo ai, ndithu pali Farao, inuyo ndinu azondi basi.” Atanena mau ameneŵa, adakaŵatsekera m'ndende masiku atatu. Patapita masiku atatu, adaŵauza kuti, “Ine ndimaopa Mulungu. Choncho ndikupatsani mwai woupulumutsa moyo wanu mukachita izi. Ngati ndinu okhulupirika, mmodzi yekha atsalire m'ndendemu, ena nonsenu mungathe kupita, kuti mukapereke tirigu mwagulayu ku banja la kwanu kuli njalako. Mng'ono wanuyo mukabwere naye kuno, kutsimikiza kuti mukunenadi zoona, ndipo simudzaphedwa.” Iwo aja adavomereza zimenezo. Ndipo adayamba kuuzana kuti, “Ndithu, ife tidalakwa pamene mng'ono wathu ankatipempha kuti timchitire chifundo, koma ife osamumvera konse chifundo. Nchifukwa chake tili m'mavuto tsopano lino.” Apo Rubeni adati, “Ine paja ndinkakuuzani kuti mnyamatuyu musamchite kanthu, inu osandimvera. Mwaonatu, tsopano tikulandira malipiro a imfa yake ija.” Yosefe anali kumva zonse zimene ankakambiranazo, koma iwowo sadadziŵe, chifukwa choti ankalankhula naye kudzera mwa womasulira. Tsono Yosefe adapita payekha kukalira misozi. Kenaka adabwerako nayambanso kulankhula nawo. Adapatulapo Simeoni, nammanga pomwepo iwowo akuwona. Tsono Yosefe adalamula kuti matumba ao adzazidwe ndi tirigu, ndipo kuti ndalama za aliyense ziikidwe m'thumba mwake momwemo. Adalamulanso kuti aŵapatse kamba wapaulendo. Antchito a Yosefe adachitadi zonsezo. Abale akewo adasenzetsa abulu ao matumba a tirigu uja adagulayu, ndipo adanyamuka ulendo. Atafika pa chigono, mmodzi mwa iwo adamasula thumba lake kuti atengeko chakudya chodyetsa bulu wake. Atamasula, adangoona kuti pakamwa pa thumbalo pali ndalama. Adaitana abale ake naŵauza kuti, “Ha, wandibwezera ndalama zanga. Si izi zili m'thumbazi.” Pamenepo onsewo mitima yao idangoti phwii! Adachita mantha kwambiri nati, “Mulungu watichita zotani ife?” Atafika kwa bambo wao Yakobe, adamsimbira zonse zimene zidaŵagwera, adati, “Nduna yaikulu ya dzikolo idatilankhula mozaza, kuti ati ndife ozonda dziko laolo. Ife tidamuuza munthuyo kuti, ‘Ndife anthu okhulupirika, osati azondi. Ife tonse tinalipo ana aamuna khumi ndi aŵiri, koma mmodzi adamwalira, ndipo wamng'ono ali ndi bambo wathu ku Kanani.’ Pamenepo iyeyo adati, ‘Kuti ndidziŵe kuti ndinu anthu okhulupirika, mmodzi mwa inu atsale ndi ine kuno, koma ena nonsenu mutenge tirigu, mupite naye ku banja la kwanu kuli njalako. Ndipo mbale wanu wamng'onoyo mudzabwere naye kuno. Pamenepo ndiye ndidzadziŵe kuti sindinu azondi, koma ndinu okhulupirika. Mbale wanuyo ndidzambwezera kwa inu. Mukadzatero mungathe kumadzachitabe malonda m'dziko muno.’ ” Atamasula matumba ao, aliyense adapeza kuti chikwama cha ndalama chinali momwe m'thumbamo. Ataona ndalamazo, iwowo pamodzi ndi bambo wao yemweyo adachita mantha kwambiri. Tsono Yakobe bambo wao adaŵauza kuti, “Mwandilanda ana anga. Yosefe adapita, ndipo nayenso Simeoni wapita, tsopano mufuna kutenganso Benjamini, zonse zandigwera ine!” Rubeni adauza atate ake kuti, “Mungathe kudzapha ana anga aŵiri, ngati Benjamini sindidzabwera naye kwa inu. Mundipatse kuti ndimsamale ndine, ndipo ndidzabwera naye.” Koma Yakobe adati, “Mwana wangayu sangapite nanu ai, paja mbale wake adamwalira, ndipo ndi yekhayu watsala. Mwina mwake angathe kuphedwa pa njira, ndipo ine m'mene ndakalambiramu, chisoni chotere chidzangonditsiriza.” Njala idakula kwambiri m'dziko la Kanani. Tsono banja la Yakobe lija litadya tirigu yense amene adaakasuma ku Ejipito uja, Yakobe adauza ana ake aja kuti, “Pitaninso, mukatigulireko chakudya pang'ono.” Apo Yuda adati, “Munthu uja adatichenjeza kolimba kuti sadzatilola kuwonekera pamaso pake, tikapanda kupita naye mng'ono wathuyu. Mukatilola kuti timtenge, tipita kukakugulirani chakudya. Mukapanda kulola, ife sitipita, popeza kuti munthu ameneyo adaneneratu kuti, ‘Sindidzakulolani kufika pamaso panga mukapanda kubwera naye mbale wanuyo.’ ” Apo Israele adati, “Chifukwa chiyani mudathinitsa zinthu pa ine pomuuza kuti muli ndi mbale wanu winanso?” Iwo adayankha kuti, “Ndiye kuti munthuyo ankangofunsitsa za ife ndi za banja lathu nkumati, ‘Kodi bambo wanu akali moyo? Kodi muli naye mbale wanu wina?’ Tsono ife tidaayenera kuyankha mafunso onseŵa. Nanga ife tikadadziŵa bwanji kuti iye atiwuza zoti mbale wathuyo tipite naye limodzi.” Yuda adauza bambo wake Israele kuti, “Mnyamatayu patsani ine, ndipo tikonzeke kuti tinyamuke tizipita. Motero tonsefe, inuyo, ana athu pamodzi ndi ife, sitidzafa ndi njala. Ine ndikhale ngati chikole cha moyo wake wa Benjamini. Ngati sindidzabwerera naye kuno ali moyo, inu mudzandiimbe mlandu moyo wanga wonse. Tikadapanda kuzengereza, tikadapita ndi kubwerako kaŵiri konse tsopano.” Tsono bambo wao Israele adaŵauza kuti, “Ngati ndi m'mene ziliri, chitani choncho. Munthuyo mtengereniko zipatso zokoma za dziko lino m'matumba mwanu kuti mukampatse. Mumtengerenso mafuta opaka pang'ono, uchi pang'ono, mafuta onunkhira osiyanasiyana, mure, mtedza, ndiponso zipatso zinanso. Mutenge ndalama zokwanira, kuti mukabweze ndalama zomwe zidapezeka m'matumba mwanu zija. Makamaka zinthu zinali zitalakwika. Mtengeni mbale wanuyu, ndipo nyamukani, mupitenso kwa munthuyo. Mulungu Mphambe akuchitireni chifundo pamaso pa munthuyo, kuti abweze mbale wanu wina uja pamodzi ndi Benjamini. Ngati ana anga onse andifera, andifera ndithu basi.” Motero abale onse aja adatenga mphatso zija, ndipo adatenganso ndalama moŵirikiza, namtenganso Benjamini. Tsono adakonzeka, nanyamuka ulendo kupita ku Ejipito. Kumeneko adakaonekera pamaso pa Yosefe. Yosefe ataona Benjamini, adauza wantchito woyang'anira zonse panyumba pake kuti, “Anthu aŵa aloŵetse m'nyumba. Ndipo uphe nyama ndi kuiphika bwino, chifukwa anthu ameneŵa adya ndi ine masana ano.” Wantchitoyo adachita monga momwe Yosefe adamuuzira, napita nawo abale aja kunyumba kwa Yosefe. Koma iwowo adachita mantha kwambiri poona kuti akupita nawo kunyumba kwa Yosefeyo: ankaganiza kuti, “Akutiloŵetsa muno chifukwa cha ndalama zija zidabwezedwa m'matumba mwathu pa nthaŵi yoyamba ija. Akungofuna danga loti achite nafe nkhondo mwadzidzidzi, chifukwa akufuna kutisandutsa akapolo ake ndi kutilanda abulu athuŵa.” Motero asanaloŵe m'nyumbamo adafika kwa wantchito wa Yosefe woyang'anira nyumba uja, namuuza kuti, “Pepani bwana, ife tidaabweranso kuno kale kudzagula chakudya. Titafika pa malo a chigono, pomasula matumba athu, aliyense mwa ife adapeza ndalama zake kukamwa kwa thumba lake, ndipo ndalamazo zinalipo zonse monga momwe tidaaŵerengera. Ndalama zimenezo tabwera nazo. Ndipo tabwera nazonso ndalama zina zodzagulira chakudya china. Amene adaika ndalama m'matumba mwathu, sitikumudziŵa ai.” Wantchito uja adati, “Musade nkhaŵa, mitima yanu ikhale pansi. Mulungu wanu, Mulungu wa atate anu, ndiye amene adakuikirani ndalama zanu m'matumbamo. Ndalama zanu zoyamba zija ndidalandira.” Atatero, adaŵatulutsira Simeoni uja. Wantchitoyo atabwera nawo abalewo m'nyumba mwa Yosefe, adaŵapatsa madzi kuti asambe mapazi ao, ndipo abulu ao aja adaŵadyetsanso. Tsono abalewo adakonzeratu mphatso zao zija kuti apereke kwa Yosefe masana, chifukwa anali atamva kuti akadya kumeneko. Yosefe atabwera, abale akewo adapereka mphatso zija kwa iye, ndipo adamuweramira. Iye adaŵafunsa m'mene aliri, naŵafunsanso kuti, “Kodi bambo wanu wokalamba uja munkandiwuzayu ali bwanji? Kodi akali moyo?” Iwowo adayankha kuti, “Mtumiki wanu akali moyo, ndipo ali bwino.” Tsono onsewo adamgwadiranso namuŵeramira pomwepo. Yosefe ataona Benjamini, mng'ono wake weniweni uja, adati “Uyu ayenera kukhala mng'ono wanu wotsiriza uja munkandiwuzayu. Mulungu akudalitse, mwana wanga.” Atanena zimenezo Yosefe adachokapo mofulumira chifukwa choti mtima wake udaadzaza ndi chifundo chifukwa cha mng'ono wake uja. Anali pafupifupi kulira, motero adapita m'chipinda mwake nakalirira m'menemo. Atapukuta m'maso adatuluka, ndipo adalimbanso mtima, nalamula kuti chakudya chibwere. Yosefe ankadyera payekha, abale akewo ankadyera pa tebulo lina. Aejipito amene anali naye m'nyumba nawonso ankadyera paokha, chifukwa iwo ankanyansidwa kudyera pamodzi ndi Ahebri. Abalewo adaakhala pa tebulo patsogolo pa Yosefe, ndipo anali ataŵaika motsatana ndi kubadwa kwao, kuyambira wamkulu mpaka wamng'ono. Abale aja ataona m'mene aŵakhazikira, adadabwa kwambiri namapenyetsetsana. Chakudya chomwe ankadyacho chinkachokera patebulo pa Yosefe, koma chakudya chopatsa Benjamini chinkaposa cha onsewo kasanu. Motero onsewo adadya ndi kumwa pamodzi ndi Yosefe mpaka kukhuta, ndipo adasangalala pamodzi naye. Pambuyo pake Yosefe adalamula wantchito wamkulu woyang'anira nyumba yake kuti, “Dzaza matumba a anthuŵa ndi chakudya chambiri momwe angathe kusenzera. Ndipo ndalama za aliyense uziike pakamwa pa thumba. Tsono pakamwa pa thumba la wamng'onoyo uikepo chikho changa chasiliva chija, pamodzi ndi ndalama zake zimene amati agulire tirigu.” Wantchitoyo adachita monga momwe adaamuuzira. M'maŵa kutacha, anthu aja adaloledwa kupita pamodzi ndi abulu ao. Atangoyenda pang'ono kuchoka mumzindamo, Yosefe adauza wantchito wake wamkulu uja kuti, “Nyamuka, uthamangire anthu aja. Ukaŵapeza, uŵafunse kuti, ‘Bwanji mwabwezera zoipa kwa zabwino? Mwaberanji chikho chimene mbuyanga amamwera? Amati akafuna kudziŵa zam'tsogolo, amagwiritsa ntchito chikho chimenechi. Ndithu zimene mwachitazi nzoipa kwambiri.’ ” Wantchito uja ataŵapeza, adanena mau omwe adaamuuza aja. Iwo aja adamuyankha kuti, “Kodi mukulankhulazi nzotani bwana? Ife sitikadatha mpang'ono pomwe kuganiza kuti tichite zimene mukunenazi. Inu nomwe mudaona kuti ife pochoka ku Kanani, tidabwera ndi ndalama zimene tidaazipeza m'matumba mwathu. Nanga tingaberenji siliva kapena golide m'nyumba mwa bwana wanu? Tsono bwana, wina mwa ife akapezeka ndi chikho chimenechi, ndithu aphedwe, ndipo tonsefe tidzakhala akapolo anu, bwana!” Apo wantchitoyo adati, “Chabwino. Komatu wina pakati panupa akapezeka ndi chikhocho, ameneyo akhala kapolo wanga, ena nonsenu muzipita mwaufulu.” Motero onsewo adatsitsa msanga matumba ao, aliyense nkumasula thumba lake. Wantchito wa Yosefe uja adafunafuna mosamala kwambiri kuyambira pa wamkulu mpaka pa wamng'ono, ndipo chikhocho adachipeza m'thumba la Benjamini. Apo onsewo adang'amba zovala zao ndi chisoni. Adasenzetsanso abulu katundu wao uja, nabwerera kumzinda konkuja. Yuda ndi abale ake atafika kunyumba kwa Yosefe, adampeza akadali momwemo ndipo onsewo adaŵerama pamaso pake. Yosefe adati, “Mwachita chiyani? Kodi simukudziŵa kuti munthu monga ine ndingathe kudziŵa zakutsogolo?” Apo Yuda adati, “Kodi ife tinganene chiyani kwa inu, bwana? Tilinso ndi mau ngati? Tingathe kudziyeretsa bwanji? Mulungu waulula cholakwa chathu, bwana. Tonsefe bwana, ndife akapolo anu, osati mmodzi yekha amene wapezeka ndi chikhoyu ai.” Koma Yosefe adati, “Iyai! Ine sindingathe kuchita zotero. Yekhayo amene wapezeka ndi chikho, ndiye adzakhala kapolo wanga. Enanu mungathe kumabwerera kwanu kwa bambo wanu.” Pamenepo Yuda adasendera kwa Yosefe, nati “Pepani bwana, loleni ine mtumiki wanu kuti ndilankhule nanu. Musati mukwiye nane bwana, inu muli ngati Farao yemwe. Bwana, paja mudaatifunsa kuti, ‘Kodi muli naye bambo wanu kapena mbale wanu?’ Ndipo ife tidaakuyankhani kuti, ‘Tili naye bambo wathu wokalamba ndi mbale wathu wina wamng'ono amene adabadwa bambo wathuyo atakalamba kale. Mkulu wake wa mnyamata ameneyo adamwalira kale. Choncho m'mimba mwa mai wake, yekhayu ndiye amene ali moyo, ndipo bambo wake amamkonda kwabasi.’ Bwana, paja inu mudaatiwuza kuti, ‘Mudzabwere naye, kuti ndidzamuwone.’ Ife tidaakuyankhani kuti, ‘Mnyamatayo sangachoke kwa bambo wake, popeza kuti akatero, bambo wakeyo kufa kudzakhala komweko.’ Tsono paja mudaanena kuti simudzatilola kufikanso pamaso panu tikadzapanda kubwera naye mng'ono wathuyo. Titabwerera kwathu kwa bambo wathu mtumiki wanu, tidamuuza mau anu onse aja. Iye atatiwuza kuti, ‘Bwererani mukatigulireko chakudya pang'ono,’ ife tidamuuza bambo wathu kuti, ‘Sitingathe kupita popeza kuti munthu uja sakatilola kufika pamaso pake, tikapanda kupita ndi mng'ono wathuyu.’ Koma bambo wathu adati, ‘Mukudziŵa kuti mkazi wanga adandibalira ana aŵiri. Wina mwa iwowo adandisiya kale. Ndiye kuti adajiwa ndi zilombo chifukwa sindidamuwonenso. Tsopano mukanditengeranso uyu, nakaphedwa, ndiye kuti ine ndidzafa ndi chisoni.’ ” Yuda adapitiriza kulankhula nati, “Nchifukwa chake tsopano ndikabwerera kwathu kwa bambo wanga, mtumiki wanu, opanda mnyamata ameneyu, amene moyo wa bambo wanga uli pa iye, akakangoona kuti iyeyu palibe, basitu akafa. Ndiye kuti ifeyo ndi amene tidzachititse bambo wathu chisoni chofa nacho mu ukalamba wake. Ndiponsotu bwana, ine ndidapereka moyo wanga kwa bambo wanga chifukwa cha mnyamata ameneyu. Ndidamuuza kuti ngati mnyamatayu sindidzabwerera naye, ndidzakhala wolakwa pamaso pa bambo wanga moyo wanga onse. Ndiye tsopano bwana, ineyo nditsalira kuno kuti ndikhale kapolo wanu m'malo mwa mnyamatayu. Muloleni iyeyu apite ndi abale akeŵa. Ine ndingathe bwanji kupita kwa bambo wanga popanda mnyamatayu kupita nane? Ine ndekha sindingathe kupirira kuti ndiwone tsoka lotere likugwera bambo wanga.” Pamenepo Yosefe sadathenso kudzigwira pamaso pa onse omtumikira aja. Adanena mokweza mau kuti, “Onse atuluke muno.” Motero panalibe ndi mmodzi yemwe wotsalira pamene Yosefe ankadziwulula kwa abale ake aja. Adalira momveka kotero kuti Aejipito adamva ndithu, ndipo mbiri ya zimenezo idakafika mpaka kwa mfumu. Yosefe adauza abale ake kuti, “Ine ndine Yosefe. Kodi bambo wanga akali moyo?” Koma abale akewo adadzazidwa ndi mantha, kotero kuti sadathenso nkumuyankha komwe. Tsono Yosefe adaŵauza kuti, “Chonde senderani pafupi.” Onse atabwera pafupi, Yosefe adati, “Ine ndine mbale wanu uja Yosefe, amene mudamgulitsa ku Ejipito. Koma tsopano musataye mtima kapena kuvutika, popeza kuti Mulungu mwiniwake ndiye amene adanditumiziratu kuno, kuti motero apulumutse moyo wanu. Chaka chino ndi chaka chachiŵiri cha njala. Koma zakhalabe zaka zisanu, ndipo pa zaka zimenezi anthu sadzalima kapena kukolola. Mulungu adanditumiziratu ine kuno kuti ndikupulumutseni, kuti choncho ziwoneke zidzukulu zanu zambiri. Motero sindinu amene mudanditumiza kuno ai, koma Mulungu. Iye wandisandutsa nduna yaikulu ya Farao. Dziko lonse lino lili m'manja mwanga. Ejipito yense ndikulamulira ndine. Tsopano fulumirani, bwererani kwa bambo wanga, mukamuuze kuti mwana wanu Yosefe akunena kuti, ‘Mulungu wandikuza mpaka kukhala wolamulira Ejipito yense, tsono bwerani kuno, musachedwe. Mungathe kudzakhala kuno ku dziko la Goseni, kuti mukhale pafupi ndi ine. Mudzakhale kuno inuyo, ana anu, zidzukulu zanu, nkhosa zanu ndi mbuzi zomwe, ng'ombe zanu pamodzi ndi zonse zimene muli nazo. Mukadzakhala ku Goseni, ine ndizidzakusamalani. Zaka za njala zikalipobe zisanu. Sindifuna kuti inu musauke pamodzi ndi banja lanu, ndi onse amene muli nawo.’ Tsono nonsenu ndi Benjamini, mng'ono wangayu, mungathe kuwona kuti ndinedi amene ndikulankhula nanu. Muuzeni bambo wanga kuti ndili pa ulemerero waukulu ku Ejipito kuno. Mukamuuzenso bambo wanga zonse zimene mwaonazi ndipo fulumirani, mubwere naye kuno.” Atatero adakumbatira Benjamini, mng'ono wake uja, nayambanso kulira. Benjamini nayenso adayamba kulira atangomkumbatira. Pambuyo pake adaŵampsompsona abale ake onse aja akulira. Kenaka abale ake aja adayamba kucheza naye Yosefe. Zitamveka kunyumba kwa Farao kuti abale a Yosefe abwera, Faraoyo ndi antchito ake onse adakondwa kwambiri. Ndipo Farao adauza Yosefe kuti, “Uŵauze abale ako kuti asenzetse nyama zao katundu, ndipo abwerere ku Kanani. Tsono kumeneko akatenge bambo wao ndi mabanja ao, ndipo adzabwere kwa ine kuno. Ndidzaŵapatsa dziko lachonde ku Ejipito kuno, ndipo azidzadya za m'dziko lino. Uŵauze kuti atenge ngolo za kuno ku Ejipito, kuti akazi ao akakwerepo pamodzi ndi ana omwe. Ndithu akamtenge bambo wao akabwere kuno. Asakade nkhaŵa kuti asiya katundu wao kumeneko, chifukwa dziko lokoma lachonde la ku Ejipito kuno lidzakhala lao.” Tsono ana a Israele adachitadi zimenezo. Yosefe adaŵapatsa ngolo monga Farao adaalamulira, naŵapatsa phoso lapaulendo. Adapatsanso aliyense zovala zachikondwerero, koma Benjamini adampatsa mashikeli asiliva okwana 300, ndi zovala zisanu zachikondwerero. Bambo wake adamtumizira abulu khumi osenza zipatso zokoma za ku Ejipito, ndi abulu khumi osenza tirigu, buledi ndi zakudya zina za bambo wake zapaulendo. Tsono adaŵauza abale akewo kuti azipita, ndipo ponyamukapo adanena kuti, “Musakangane pa njira.” Tsono iwo adachoka ku Ejipito, kubwerera ku Kanani kwa bambo wao Yakobe. Atafika, adauza bambo wao kuti, “Yosefe ujatu ali moyo! Ndiye wolamulira Ejipito yense!” Yakobe adachita ngati wakomoka, pakuti sadakhulupirire zonena zaozo. Komabe iwo atamuuza zonse zimene Yosefe adaaŵauza, ndipo iye ataona ngolo zimene Yosefe adaatumiza kuti iye akwerepo popita ku Ejipito, Yakobe adayamba kutsitsimuka. Tsono adati, “Basi chabwino, mwana wanga Yosefe akali moyo. Ndipita ndikamuwone ndisanafe.” Israele adasonkhanitsa zake zonse napita ku Beereseba kukapereka nsembe kwa Mulungu wa atate ake Isaki. Usiku Mulungu adaonekera Israele m'masomphenya, ndipo adati, “Yakobe, Yakobe!” Iye adayankha kuti, “Ee Ambuye!” Ndipo adamuuza kuti “Ine ndine Mulungu, Mulungu wa atate ako. Usaope kupita ku Ejipito. Kumeneko ndidzachulukitsa zidzukulu zako, kuti zikhale mtundu waukulu wa anthu. Ineyo ndidzapita nawe ku Ejipito, ndipo zidzukulu zakozo ndidzazibwezeranso konkuno. Yosefe adzakhala nawe pa nthaŵi yako yomwalira.” Tsono Yakobe adanyamuka kuchoka ku Beereseba. Ana ake a Israele aja adakweza bambo wao Yakobe, pamodzi ndi akazi ndi ana, pa ngolo zimene Farao adaatumiza. Adatenga zoŵeta zao zonse pamodzi ndi zinthu zonse zimene anali nazo ku Kanani, ndipo adapita ku Ejipito. Yakobe adatenga zidzukulu zake zonse, ndiye kuti ana ndi adzukulu ake aamuna, ndiponso ana ndi adzukulu ake aakazi. Onsewo adapita nawo ku Ejipito. Naŵa maina a Aisraele amene adapita ku Ejipito, ndiye kuti Yakobe ndi ana ake. Rubeni, mwana wachisamba wa Yakobe, ndi ana aŵa a Rubeni: Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karimi. Ana a Simeoni anali aŵa: Yemuwele, Yamini, Ohadi, Yakini, Zohari ndi Shaulo, amene mai wake anali mkazi wa ku Kanani. Ana a Levi anali aŵa: Geresoni, Kohati ndi Merari. Ana a Yuda anali aŵa: Ere, Onani, Sela, Perezi ndi Zera, (koma Ere ndi Onani adaafera ku Kanani.) Ana a Perezi anali aŵa: Hezironi ndi Hamuli. Ana a Isakara anali aŵa: Tola, Puva, Iyobu ndi Simironi. Ana a Zebuloni anali aŵa: Seredi, Eloni ndi Yaleele. (Ana ameneŵa ndiwo amene Leya adabalira Yakobe ku Mesopotamiya kuja, ndipo panalinso mwana wake wamkazi Dina. Adzukulu obadwa mwa Leya analipo 33 onse pamodzi.) Ana a Gadi anali aŵa: Zifiyoni, Hagi, Suni, Eziboni, Eri, Arodi ndi Areli. Ana a Asere anali aŵa: Imina, Isiva, Isivi, Beriya ndi mlongo wao Sera. Ana a Beriya anali aŵa: Hebere ndi Malikiele. (Onseŵa anali adzukulu a Yakobe obadwa mwa Zilipa amene Labani adaapereka kwa mwana wake Leya.) Ana a Rakele mkazi wa Yakobe anali aŵa: Yosefe ndi Benjamini. Manase ndi Efuremu anali ana amene Yosefe adabereka mwa Asenati, mwana wa Potifera wansembe wa ku Oni. Ana a Benjamini anali aŵa: Bela, Bekara, Asibele, Gera, Naamani, Ehi, Rosi, Mupimu, Hupimu ndi Aridi. (Onseŵa 14 ndiwo adzukulu a Yakobe mwa mkazi wake Rakele.) Dani anali ndi mwana mmodzi yekha dzina lake Husimu. Ana a Nafutali anali aŵa: Yazeele, Guni, Yezera ndi Silemu. (Asanu ndi aŵiriŵa ndiwo adzukulu a Yakobe amene adabadwa mwa Biliha, amene Labani adaapereka kwa mwana wake Rakele.) Chiŵerengero chonse cha anthu ochokera mwa Yakobe, amene adapita ku Ejipito, chinali 66, osaŵerengera akazi a ana ake. Popeza kuti Yosefe adaabereka ana aŵiri ku Ejipito, chiŵerengero chidafika 70. Onseŵa anali a m'banja la Yakobe, ndipo ndiwo adapita ku Ejipito. Israele adatuma Yuda kuti atsogole kupita kwa Yosefe kukampempha kuti akamchingamire ku dziko la Goseni. Yakobe atafika ku dziko la Goseni, Yosefe adaitanitsa galeta lake, napita ku Goseni kukakumana ndi Israele bambo wake. Atangofika pamaso pake, adamkumbatira m'khosi, nalira nthaŵi yaitali ndithu, osalekerapo. Israele adauza Yosefe kuti, “Tsopano ndimwalire, popeza kuti ndakuwona, ndipo ndikudziŵadi kuti uli moyo.” Apo Yosefe adauza abale ake aja pamodzi ndi banja lonse la bambo wake kuti “Ndipita ndikamuuze Farao kuti abale anga pamodzi ndi onse a m'banja la atate anga amene ankakhala ku Kanani, abwera kuno kwa ine. Anthu ameneŵa ndi abusa, amaŵeta zoŵeta. Nkhosa zao ndi ng'ombe zomwe abwera nazo, pamodzi ndi zinthu zao zonse. Tsono Farao akakuitanani, ndipo akakufunsani kuti, ‘Mumagwira ntchito yanji?’ Inu mukamuuze kuti, ‘Ife bwana, ndife oŵeta zoŵeta kuyambira ubwana wathu, monga momwe ankachitira makolo athu.’ Mukatero, ndiye kuti mudzatha kukakhala m'dziko la Goseni.” Yosefe adaanena zimenezi chifukwa choti Aejipito ankanyansidwa ndi abusa. Tsono Yosefe adatenga abale ake asanu napita nawo kwa Farao kukamuuza kuti, “Bambo wanga pamodzi ndi abale anga abwera kuchokera ku Kanani. Abwera ndi zoŵeta zao monga nkhosa ndi ng'ombe, pamodzi ndi zao zonse. Tsopano akukhala m'dziko la Goseni.” Aŵa ndi asanu mwa abale angawo. Apo Farao adaŵafunsa kuti, “Kodi mumagwira ntchito yanji?” Iwo adayankha kuti, “Ndife abusa bwana, monga momwe ankachitira makolo athu.” “Tabwera kudzakhala nao m'dziko muno bwana, chifukwa ku Kanani kuli njala yoopsa, kotero kuti kulibe ndi msipu womwe wodyetsa zoŵeta. Chonde bwana, mutilole tikakhale ku dziko la Goseni.” Tsono Farao adauza Yosefe kuti, “Bambo wako pamodzi ndi abale ako abwera kwa iwe. Dziko la Ejipito lili m'manja mwako. Ukhazike bambo wako pamodzi ndi abale ako m'dziko lachonde, akakhale ku Goseni. Ndipo ngati ena mwa iwo ndi akatswiri a zoŵeta, uŵapatse ukapitao woyang'anira zoŵeta zanga.” Yosefe adatenga bambo wake Yakobe, napita naye kwa Farao. Ndipo Yakobe adadalitsa Faraoyo. Kenaka Farao adafunsa Yakobe kuti, “Muli ndi zaka zingati?” Yakobe adayankha kuti, “Zaka za maulendo anga zakwana 130. Zaka zimenezi nzochepa ndiponso zamavuto, zosalingana ndi zaka za makolo anga pa nthaŵi yao yonse pamene anali moyo.” Ndipo atadalitsa Farao, adatsazikana naye nkuchokapo. Yosefe adamkhazika m'dziko la Ejipito bambo wake uja, pamodzi ndi abale ake onse aja, ndipo adaŵapatsa malo a nthaka yabwino ndi yachonde, m'chigawo chotchedwa Ramsesi, monga momwe Farao adaalamulira. Yosefe adapereka chakudya kwa bambo wake ndi kwa abale ake ndi kwa mbumba yonse, potsata kuchuluka kwa ana ao. Njala ija idakula kwambiri, kotero kuti panalibe chakudya pa dziko lonse lapansi, ndipo anthu a ku Ejipito ndi a ku Kanani komwe adafooka nayo njalayo. Yosefe adasonkhanitsa ndalama zonse zimene anthu a ku Ejipito pamodzi ndi a ku Kanani adaamwaza pogula tirigu. Ndalama zonsezo adazitenga napita nazo kunyumba kwa Farao. Ndalama zonse zitaŵathera anthu a ku Ejipito ndi a ku Kanani, Aejipito ambiri adabwera kwa Yosefe, namuuza kuti, “Tipatseniko chakudya! Musatilekerere kuti tife, chitanipo kanthu! Ndalama zathu zonse zatha!” Yosefe adaŵayankha kuti “Bwerani ndi zoŵeta zanu, tidzasinthane ndi chakudya, ngati mukuti ndalama zanu zidatha zonse.” Motero adabwera ndi zoŵeta zao kwa Yosefe, nasinthitsa ndi chakudya zoŵeta zaozo, monga akavalo, nkhosa ndi mbuzi, ng'ombe ndi abulu. Chaka chimenecho Yosefe adaŵapatsa chakudya anthuwo mosinthana ndi zoŵeta zaozo. Chitatha chaka chimenecho, anthuwo adapitanso kwa Yosefe namuuza kuti, “Bwana, ife sitingakubisireni kuti ndalama zathu pamodzi ndi zoŵeta zathu zomwe, zatithera. Palibe chilichonse chotsala choti tingathe kukupatsani, tingodzipereka ifeyo ndi minda yathuyi. Musatilekerere kuti tife m'dziko mwathu, inu mukuwona. Mutipatseko chakudya, ndipo tidzigulitsa ifeyo ndi minda yathu yomwe. Tidzakhala akapolo a Farao, iye adzatenga minda yathu kuti ikhale yake. Mutipatseko mbeu kuti tisafe ndi njala, kutinso minda yathu isakhale masala.” Apo Yosefe adagulira Farao dziko lonse la Ejipito. Mwejipito aliyense adagulitsa minda yake chifukwa njalayo inali itafika poipa kwambiri. Motero dziko lonse lidasanduka la Farao. Yosefe adaŵasandutsa akapolo anthuwo ponseponse m'dziko la Ejipito. Dziko limene sadagule ndi la ansembe lokha. Iwowo sadagulitse dziko lao, popeza kuti Farao ankaŵapatsa chakudya choti azidya. Yosefe adauza anthu kuti, “Onani tsopano ndakugulani pamodzi ndi minda yanu yonse, kugulira Farao. Tsono nazi mbeu, mubzale m'minda mwanu. Pa nthaŵi yokolola mudzapereka kwa Farao chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse pa zokolola zanuzo, ndipo zina zonse zotsala zidzakhala zanu. Zina mudzasungire mbeu, koma zina mudzadye inuyo, mabanja anu ndi antchito anu.” Anthu adayankha kuti, “Mwapulumutsa moyo wathu. Mwatichitira zabwino bwana, tidzakhala akapolo a Farao.” Motero Yosefe adapanga lamulo m'dziko lonse la Ejipito, kuti chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse pa zokolola chidzakhala cha Farao. Lamulo limeneli lilipobe mpaka lero lino. Koma maiko a ansembe okha sadaŵatenge kuti akhale a Farao. Aisraele atakhazikika ku Ejipito, adalemera kwambiri, ndipo adaberekanso ana ambiri. Yakobe adakhala ku Ejipito, zaka 17, choncho zaka za moyo wake zidakwanira 147. Tsono ali pafupi kumwalira, adaitana mwana wake Yosefe namuuza kuti, “Ngati ukundikondadi, undigwire m'kati mwa ntchafu zangazi, ulonjeze kuti udzandikomera mtima ndi kukhulupirika kwa ine, ndipo kuti mtembo wanga sudzauika ku Ejipito kuno. Ndifuna kukagona pamodzi ndi makolo anga. Mtembo wanga udzauchotse ku Ejipito kuno ukauike m'manda a makolo anga.” Yosefe adayankha kuti, “Ndidzachita monga momwe mwaneneramu.” Yakobe adauzanso Yosefe kuti, “Lumbira pamaso panga kuti udzachitadi zimenezi.” Apo Yosefe adalumbiradi, ndipo Yakobe adaŵerama kumutu kwa bedi lake. Patapita kanthaŵi, Yosefe adamva kuti “Bambo wanu akudwala.” Adatenga ana ake aŵiri, Manase ndi Efuremu, napita nawo kwa Yakobe. Yakobeyo atamva kuti “Mwana wanu Yosefe wabwera kudzakuzondani,” adadzilimbitsa, nadzuka, nkukhala tsonga pabedi pompo. Adauza Yosefe kuti, “Mulungu Mphambe amene adandiwonekera ku Luzi m'dziko la Kanani, adandidalitsa. Adandiwuza kuti, ‘Ndidzakupatsa ana ambiri kotero kuti zidzukulu zako zidzasanduka mitundu yambiri ya anthu. Dziko lino ndidzapatsa zidzukulu zako kuti likhale lao mpaka muyaya.’ Tsono ana ako aŵiri, amene udabereka ku Ejipito kuno, ine ndisanabwere, amenewonso ndi anga. Efuremu ndi Manase adzakhala anga ndithu, monga momwe aliri Rubeni ndi Simeoni. Koma obadwa pambuyo pa iwowo, ndi ako amenewo. Adzalandira choloŵa chao pamodzi ndi achibale ao. Ndachita zimenezi chifukwa chakuti pamene ndinkabwerera kuchokera ku Mesopotamiya, mai wako Rakele adafera m'dziko la Kanani, mtunda wofika ku Efurata ukadalipo. Chisoni changa chinali chachikulu. Tsono ndidamuika komweko pa mseu wa ku Efurata ku Betelehemu.” Yakobe ataona ana a Yosefe, adafunsa kuti, “Nanga anyamata aŵa nga yani?” Yosefe adayankha kuti “Ameneŵa ndi ana anga amene Mulungu adandipatsa ku Ejipito kuno.” Apo Yakobe adati, “Chonde abwere kuno anawo kuti ndiŵadalitse.” Maso a Yakobe sankapenya bwino chifukwa cha ukalamba. Yosefe adabwera nawo kwa iye anawo ndipo Yakobe adaŵakumbatira, naŵampsompsona. Yakobe adauza Yosefe kuti, “Sindinkayembekeza kuti ndingakuwonenso, koma tsopano Mulungu wandilola kuti ndiwone ndi ana ako omwe.” Tsono Yosefe adatenga anawo kuŵachotsa pa maondo a Yakobe. Ndipo adamgwadira. Yosefe adaŵagwira padzanja anawo, Efuremu ku dzanja lamanja kuti pakutero akhale ku dzanja lamanzere la Yakobe. Manase adakhala kumanzere kuti pakutero akhale ku dzanja lamanja la Yakobe. Koma Yakobe adasemphanitsa manja. Motero adasanjika dzanja lake lamanja pamutu pa Efuremu amene anali wamng'ono, dzanja lamanzere adalisanjika pamutu pa Manase amene anali wamkulu. Ndipo adadalitsa Yosefe ndi mau akuti, “Mulungu amene makolo anga Abrahamu ndi Isaki adamtumikira, Mulungu amene wanditsogolera moyo wanga wonse mpaka lero lino, aŵadalitse anaŵa! Mngelo amene wandiwombola ku zoipa zonse, aŵadalitsenso! Podzera mwa anaŵa, dzina langa ndi maina a makolo anga Abrahamu ndi Isaki akhale omveka nthaŵi zonse! Adzakhale ndi ana ambiri iwoŵa, adzasanduke mtundu waukulu pa dziko lapansi!” Yosefe ataona kuti bambo wake wasanjika dzanja lamanja pamutu pa Efuremu, adakhumudwa. Motero adatenga dzanja la bambo wake kulichotsa pamutu pa Efuremu, nalisanjika pamutu pa Manase. Adauza bambo wake kuti, “Musatero atate. Wamkulu ndi uyu. Dzanja lanu lamanja likhale pamutu pa ameneyu.” Koma bambo wakeyo adakana nati, “Ndikudziŵa, mwana wanga, ndikudziŵa. Adzukulu a Manase adzakhalanso anthu otchuka, koma mng'ono wakeyu adzatchuka kupambana iye, ndipo zidzukulu zake zidzakhala mitundu yaikulu ya anthu.” Motero adaŵadalitsa pa tsiku limenelo ndi mau akuti, “Aisraele adzatchula maina anu podalitsa. Adzanena kuti, ‘Mulungu akudalitseni inu monga Efuremu ndi Manase.’ ” Mwa njira imeneyi adaika Efuremu patsogolo pa Manase. Pambuyo pake Yakobe adauza Yosefe kuti, “Ukuwonatu kuti ndili pafupi kufa, koma Mulungu adzakhala nawe, ndipo adzakubweza ku dziko la makolo ako. Ndiponso iweyo, osati abale ako, ndikukupatsa Sekemu, dera lija limene ndidachita cholanda ndi lupanga langa ndi uta wanga kwa Aamori.” Pambuyo pake Yakobe adaitana ana ake naŵauza kuti, “Sonkhanani pamodzi, kuti ndikuuzeni zimene zidzakuchitikireni m'tsogolo muno. “Bwerani kuno, ndipo mumve, inu ana a Yakobe, mverani bambo wanu Israele. “Rubeni mwana wanga wachisamba, ndiwe nkhongono zanga, ndiwe mphatso yoyamba ya mphamvu zanga. Mwa ana anga onse, wopambana ndiwe pa ulemerero ndi mphamvu. Uli ngati chigumula cha madzi oopsa, koma sudzakhalanso wopambana, chifukwa chakuti sudaope kugona pa bedi la ine bambo wako. Udaloŵa m'bedi langa, nuliipitsa! “Simeoni ndi Levi mpachibale pao, amagwiritsa ntchito zida zankhondo pochita chiwawa. Ine sindidzakhala nao pa zokambirana zao zam'seri, sindifuna kukhala nao m'misonkhano yao, chifukwa choti adapha anthu mokalipa, ndipo adapundula ng'ombe zamphongo mwankhanza, naziyesa choseketsa. Matemberero aŵagwere, chifukwa mkwiyo wao ndi woopsa kwambiri, ukali wao utembereredwenso, chifukwa imeneyo ndi nkhalwe. Ndidzaŵamwaza iwowo m'dziko lonse la Yakobe. Ndidzaŵabalalitsa pakati pa Israele. “Iwe Yuda, abale ako adzakutamanda. Adani ako udzaŵagwira pa khosi, abale ako adzakugwadira iwe. Yuda ali ngati msona wa mkango. Ukapha, umabwereranso kumalo kumene umabisala. Yuda ali ngati mkango, amatambasuka nagona pansi. Iye ndi mkangodi, ndipo palibe amene angalimbe mtima kuti amdzutse. Ndodo yaufumu siidzachoka mwa Yuda, adzachita kuupanira ufumu umenewo, adzasunga mphamvu zake, mpaka mwiniwake weniweni atabwera, wodzalamulira anthu onse. Bulu wake amamumangirira ku mtengo wamphesa, mwanawabulu ku mpesa wabwino. Zovala zake amazichapa mu vinyo, mu vinyo wofiira ngati magazi. Maso ake ndi ofiira ndi vinyo mano ake ndi oyera ndi mkaka. “Zebuloni adzakhala m'mbali mwa nyanja, madooko ake adzakhala malo a zombo, dziko lake lidzafika mpaka ku Sidoni. “Isakara ali ngati bulu wamphamvu, amagona chotambasuka pakati pa makola. Ataona kukoma kwa malo ousirapowo, ndi kukongola kwa dzikolo. Adaŵeramitsa msana kuti anyamule katundu wake, ndipo adasanduka womagwira ntchito yaukapolo. “Dani adzalamulira anthu ake. Anthuwo adzalingana ndi mafuko ena a Israele. Dani adzakhala ngati njoka pambali pa mseu, njoka yaululu ndithu m'mbali mwa njira, yoluma ku chidendene cha kavalo, kotero kuti wokwerapo wake adzagwa chagada. “Ndikuyembekeza chipulumutso chanu, Inu Chauta. “Gadi anthu achifwamba adzamthira nkhondo, koma iyeyo adzaŵatembenukira nkuŵapirikitsa. “Dziko la Asere lidzabala chakudya chokoma, choyenera kudya mafumu. “Nafutali ali ngati insa yongoyenda mwaufulu, imene imabala ana okongola. “Yosefe ali ngati nthambi yobala zipatso, nthambi yobala zipatso pafupi ndi kasupe, nthambi yotambasuka pa khoma. Adani ake adalimbana naye mwankhalwe, namthamangitsa ndi mauta ao. Koma iyeyo uta wake sudagwedezeke, mikono yake idalimbika, ndi mphamvu za Mulungu Wamphamvuzonse wa Yakobe, amene ali Mbusa ndi Thanthwe la Israele. Ndi Mulungu wa atate ako amene amakuthandiza, ndi Mulungu Mphambe amene amakudalitsa. Amakudalitsa ndi mvula yochokera mu mlengalenga, ndi madzi otumphuka pansi pa nthaka, ndipo adzakudalitsa pakukupatsa ana ambiri ndi ng'ombe zambiri. Madalitso a bambo wako ndi amphamvu kupambana madalitso a mapiri amuyaya, kupambananso zabwino za ku zitunda zamuyaya. Zimenezi zidzakhala pamutu pa Yosefe, pamphumi pa kalonga amene adampatula pakati pa abale ake. “Benjamini ali ngati mmbulu wolusa umene m'maŵa umapha ndi kudya zimene udagwira, ndipo madzulo umagaŵa zimene udagwirazo.” Aŵa ndiwo akulu a mafuko khumi ndi aŵiri a Aisraele, ndipo zimenezi nzimene bambo wao Yakobe adaŵauza, pamene ankadalitsa aliyense mwa iwo potsazikana nawo. Tsono Yakobe adaŵalamula ana akewo kuti, “Popeza kuti tsopano ndilikufa, mukandiike m'phanga limene lili m'munda wa Efuroni Muhiti, ku Makipera. Lili kuvuma kwa Mamure m'dziko la Kanani. Abrahamu adaagula phangalo pamodzi ndi munda womwe kwa Efuroni Muhiti, kuti pakhale manda. Kumeneko ndiko kumene adaika Abrahamu pamodzi ndi Sara mkazi wake. Isaki pamodzi ndi mkazi wake Rebeka, adaŵaikanso komweko, ndipo Leya ndidamuika komwekonso. Mundawo pamodzi ndi phangalo adagula kwa Ahiti.” Tsono Yakobe atamaliza kulangiza ana ake, adabwezeranso mapazi ake m'bedi ndipo adamwalira. Pomwepo Yosefe adadzigwetsa pa mtembo wa bambo wake akulira, kwinaku akumpsompsona bambo wake. Tsono Yosefeyo adalamula asing'anga kuti akonze ndi mankhwala mtembo wa bambo wake, kuti usaole, ndipo iwowo adachitadi zimenezo. Ntchitoyo idaŵatengera masiku 40, monga kunkafunikira pa ntchito ya mtundu umenewo. Aejipito adalira maliro a Israele masiku 70. Yosefe atatha kulira maliro a bambo wake, adauza nduna za Farao kuti, “Chonde mundikomere mtima, Farao mukamuuze kuti, ‘Pamene bambo wanga anali pafupi kufa, adandilumbiritsa kuti ndikamuike m'manda amene adadzikumbira m'dziko la Kanani. Motero chonde, mundilole kuti ndipite ndikaike bambo wanga, pambuyo pake ndidzabweranso.’ ” Farao adamuyankha kuti, “Pita ukaike atate ako monga momwe adakulumbiritsira.” Yosefe adapita kukaika bambo wake. Ndipo nduna zonse za Farao, akuluakulu a bwalo, ndi anthu ena otchuka a ku Ejipito adamperekeza. Adapitanso ndi onse a banja lake, abale ake, ndi onse a banja la bambo wake. Ku Goseni kuja kudangotsala ana okhaokha, nkhosa zao, abusa ndi ng'ombe zao. Asilikali okwera pa magaleta ndi akavalo, nawonso adamperekeza. Motero chinali chinamtindi cha anthu. Atafika ku malo opunthira tirigu ku Atadi, kuvuma kwa Yordani, adachita mwambo waulemu wamaliro, ndipo adalira maliro kumeneko masiku asanu ndi aŵiri. Tsono nzika za ku Kanani zitaona kulira koteroko ku Atadi kuja, zidati, “Kulira kwa maliro kotereku ndi kwa ku Ejipito.” Nchifukwa chake malowo adaŵatchula kuti Abele-Miziraimu, ali kuvuma kwa Yordani. Ana a Yakobe adachitadi monga momwe bambo wao adaaŵalamulira. Adamnyamula kupita ku Kanani, nakamuika m'phanga limene linali m'munda ku Makipera, kuvuma kwa Mamure. Abrahamu adagula phangalo kwa Efuroni Muhiti pamodzi ndi munda womwewo, kuti pakhale manda. Yosefe ataika bambo wake m'manda, adabwerera ku Ejipito ndi abale ake aja, pamodzi ndi onse amene adamperekeza. Atamwalira bambo wao uja, abale ake a Yosefe adati, “Nanga tidzatani ife, Yosefe akadzayamba kudana nafe ndi kufuna kubwezera zoipa zonse zimene tidamuchita zija?” Motero adatumiza mau kwa Yosefe kuti, “Atate anu asanafe adanena mau akuti, ‘Ndikumpempha Yosefe kuti akhululukire cholakwa cha abale ake chimene adamchitira.’ Pepani tsopano tikhululukireni cholakwa chimene ife, akapolo a Mulungu wa atate anu, tidachita.” Atangomva zimenezi Yosefe adayambapo kulira. Tsono abale ake adabwera nagwada pamaso pake. Adati, “Ife tili pamaso panu ngati akapolo anu.” Koma Yosefe adaŵauza kuti, “Musaope ai. Ine sindingathe kudziika m'malo mwa Mulungu. Inu mudaapangana kuti mundichite chiwembu, koma Mulungu adazisandutsa kuti zikhale zabwino ndipo kuti zipulumutse moyo wa anthu ambiri. Choncho onsewo ali moyo lero lino chifukwa cha zimenezo. Tsopano inu musade nkhaŵa. Ndidzakusamalani pamodzi ndi ana anu omwe.” Motero adaŵalimbitsa mtima naŵasangulutsa. Yosefe adakhala ku Ejipito pamodzi ndi mbumba ya atate ake. Pamene ankamwalira nkuti ali wa zaka 110. Adakhala moyo mpaka kuwona adzukulu ake, ana a Efuremu. Pamene ana a Makiri mwana wa Manase adabadwa, Yosefe adaŵalandira m'banja mwake. Ndipo adauza abale ake aja kuti, “Patsala pang'ono kuti ndikusiyeni, koma Mulungu adzakusungani ndithu, ndipo adzakutulutsani m'dziko muno, kupita nanu ku dziko limene adaalonjeza Abrahamu, Isaki ndi Yakobe.” Kenaka Yosefe adapempha ana a Israele kuti alumbire. Adati, “Lonjezeni kuti Mulungu akakusungani, mudzasenza mafupa anga kuchoka nawo kuno.” Motero Yosefe adamwalira ali wa zaka 110. Mtembo wake adaukonza ndi mankhwala, naukhazika m'bokosi ku Ejipito komweko. Naŵa ana a Yakobe amene adapita ku Ejipito pamodzi ndi Yakobeyo ndi mabanja ao omwe: Rubeni, Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, Zebuloni, Benjamini, Dani, Nafutali, Gadi ndi Asere. Chiŵerengero chenicheni cha anthu obadwa mwa Yakobe chinali makumi asanu ndi aŵiri. Yosefe anali atakhazikika kale ku Ejipito. Tsono Yosefe adamwalira, abale ake ndi mbadwo wao wonse uja adamwaliranso. Koma adzukulu a Aisraele adabala ana ambirimbiri. Adachulukana nakhala amphamvu kwambiri nkudzaza dzikolo. Pambuyo pake padaloŵa mfumu ina imene sidadziŵe za Yosefe. Mfumuyo idauza anthu ake kuti, “Aisraeleŵa akuchuluka kwambiri, ndipo ndi amphamvu kupambana ife. Mvetsani tsono, ife tichite nawo mwanzeru anthu ameneŵa. Tiŵachenjerere, kuti asachuluke, chifukwatu pa nthaŵi ya nkhondo, iwoŵa angathe kudzaphatikizana ndi adani athu, nadzalimbana nafe, kenaka nkudzachoka m'dziko mwathu muno.” Tsono adaika akapitao ao oŵagwiritsa mwankhanza ntchito yolimba Aisraelewo, kuti pakutero aŵafooketse. Aisraele adamangira Faraoyo mizinda ya Pitomu ndi Ramsesi, kumene Aejipito ankasunga chakudya chao. Koma Aisraele ankati akamaŵazunza kwambiri, ndi pamene iwo tsono ankachulukirachulukira, mpaka adabalalikira m'dziko lonselo. Motero Aejipito ankaŵaopa Aisraele, ndipo ankaŵakakamiza mwankhalwe kugwira ntchito yaukapolo. Moyo wa Aisraele unali woŵaŵa chifukwa cha ntchito yakalavulagaga youmba njerwa, ndiponso ntchito zosiyanasiyana zam'minda. Ankaŵakakamiza mwankhanza kugwira ntchito zonse zolemetsa. Tsono mfumu ya ku Ejipito ija idaitana azamba amene ankathandiza azimai achihebri pochira. Wina mwa azamba ameneŵa anali Sifira, wina anali Puwa. Mfumuyo idauza azambawo kuti, “Mukamathandiza azimai achihebri pochira, akabadwa mwana wamwamuna, mupheni, akakhala wamkazi, mlekeni.” Koma azambawo ankaopa Mulungu, kotero kuti mau a mfumu aja sadaŵasamale konse, ana aamunawo ankangoŵaleka amoyo. Tsono mfumu ija idaŵaitana azamba aja niŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mwaŵaleka ana aamuna osaŵapha?” Azamba aja adayankha kuti “Azimai achihebri safanafana ndi azimai achiejipito. Iwo ngamphamvu, amati mzamba asanafike, mwana amakhala atabadwa kale.” Choncho Mulungu adaŵakomera mtima azambawo, mwakuti Aisraele adapitirirabe kuchulukana, nakhala amphamvu kwambiri. Tsono chifukwa choti azambawo ankaopa Mulungu, Mulungu adaŵapatsa mabanja. Pamenepo Farao adalamula anthu ake kuti, “Mwana aliyense wamwamuna wobadwa mwa Ahebri azimponya mu mtsinje wa Nailo, koma ana onse aakazi aziŵaleka, azikhala moyo.” Munthu wina wa fuko la Levi adakwatira mkazi wa fuko lomwelo. Mkaziyo adatenga pathupi, nabala mwana wamwamuna. Ataona kuti mwanayo ndi wokongola, adamubisa miyezi itatu. Koma mwanayo atafika pa msinkhu woti sangathe kumubisanso, maiyo adatenga kadengu kabango, nakamata phula. Tsono mwanayo adamuika m'menemo, nakabisa kadenguko pakati pa bango lalitali m'madzi, pafupi ndi chibumi cha mtsinjewo. Ndipo mlongo wake wa mwanayo adaimirira pafupi namangopenyetsetsa, kuti aone zimene zimchitikire mwanayo. Nthaŵi ina mwana wamkazi wa Farao adapita kumtsinje komweko kukasamba. Iyeyo anali ndi adzakazi ake, ndipo onsewo ankangoyenda m'mbali mwa mtsinje muja. Tsono mwana wa Farao uja adakaona kadengu kaja m'bangomo, natuma mdzakazi wake kuti akakatenge. Atakatsekula kadengu kaja, adapezamo kamwana kakamuna kakungolira. Mtsikanayo adachita nako chifundo kamwanako, ndipo adati, “Kameneka ndi kamwana kachihebri.” Apo mlongo wake wa mwanayo adafunsa kuti, “Bwanji ndikakuitanireni mai wachihebri woti akakulerereni mwanayu?” Mwana wa Farao uja adayankha kuti, “Chabwino, pita.” Mlongo wakeyo adapita nakaitana amai ake a mwanayo. Tsono mwana wa Farao uja adauza maiyo kuti, “Mtengeni mwanayu, mukandilerere, ine ndidzakulipirani.” Motero mai uja adamtenga mwanayo, nakamlera. Mwana uja atakula adakampereka kwa mwana wa Farao, ndipo adasanduka mwana wake ndithu. Mwana wa Faraoyo adamutcha Mose, chifukwa adati, “Ndidamuvuula m'madzi.” Tsiku lina Mose, atakula ndithu, adapita kukacheza kwa anthu a mtundu wake uja, ndipo adaona m'mene ankaŵagwiritsira ntchito moŵazunza kwambiri. Adaona Mwejipito wina akumenya Muhebri, mmodzi mwa anthu a mtundu wake. Pamenepo Mose atayang'ana uku ndi uku, naona kuti kulibe anthu, adamupha Mwejipitoyo, nafotsera mtembo wake mu mchenga. M'maŵa mwake atabweranso, adaona kuti Ahebri aŵiri akumenyana. Mose adafunsa wolakwayo kuti, “Chifukwa chiyani ukumumenya mnzako?” Iye uja adafunsa Mose kuti, “Kodi ndani adakuika kuti uzitilamula ndi kumatiweruza? Kodi ukufuna kundipha monga muja udaphera Mwejipito uja?” Pamenepo Mose adachita mantha kwambiri naganiza mumtima mwake kuti, “Ha, anthu akudziŵa zimene ndidachita zija!” Tsono Farao atamva, adayesetsa kuti aphe Mose, koma Mose adathaŵa nakakhala ku dziko la Midiyani. Ali kumeneko, tsiku lina adakhala pansi pafupi ndi chitsime. Amene anali wansembe ku Midiyaniko anali ndi ana aakazi asanu ndi aŵiri. Ana aakaziwo adabwera kudzatunga madzi, kuti adzaze m'chomwera nkhosa ndi mbuzi za bambo wao. Koma kudabwera abusa ena naŵapirikitsa atsikanawo. Apo Mose uja adaimirira naŵathandiza atsikana aja, ndipo adamwetsa zoŵeta zao zonse zija. Atsikana atabwerera kwa bambo wao Reuele, bambo waoyo adaŵafunsa kuti, “Bwanji mwabwerako msanga chotere lero?” Iwo aja adayankha kuti, “Mwejipito wina ndiye amene watitchinjiriza kwa abusa, ndipo watitungira madzi omwetsa zoŵeta zonsezi.” Tsono bambo waoyo adaŵafunsa kuti, “Nanga iyeyo ali kuti? Chifukwa chiyani mwamsiya komweko munthu ameneyo? Pitani mukamuitane, adzadye nao kuno.” Choncho Mose adavomera kukhala nao komweko, ndipo Reuele adapatsa Moseyo mwana wake Zipora kuti akhale mkazi wake. Zipora adabala mwana wamwamuna. Pamenepo Mose adati, “Ndine mlendo m'dziko lachilendo.” Motero adamutcha mwanayo Geresomo. Patapita nthaŵi yaitali ndithu, mfumu ya ku Ejipito ija idamwalira. Monsemo Aisraele ankangolira nawo ukapolo wao uja, namapempha chithandizo, ndipo kulira kwao kudamveka kwa Mulungu. Mulungu adamva kudandaula kwaoko, nakumbukira chipangano chake chija chimene adachita ndi Abrahamu, Isaki ndi Yakobe. Mulungu ataŵapenya Aisraelewo, adaŵamvera chifundo. Mose ankaŵeta ziŵeto za mpongozi wake Yetero, wansembe uja wa ku Midiyani. Tsiku lina adatenga ziŵetozo, nayenda nazo cha kuzambwe kwa chipululu, mpaka kukafika ku phiri la Mulungu dzina lake Horebu. Mngelo wa Chauta adamuwonekera ngati malaŵi a moto umene unkayaka m'chitsamba. Mose atapenya, adaona kuti chitsamba chili moto laŵilaŵi, koma osapsa. Tsono mumtima mwake adati, “Ndipita pafupi, kuti ndikaonetsetse zozizwitsa ndikupenyazi. Chifukwa chiyani chitsambacho sichilikupsa?” Chauta ataona kuti Mose akuyandikira, adamuitana m'chitsambamo kuti, “Mose, Mose!” Mose adayankha kuti “Ŵaŵa.” Mulungu adati, “Usayandikire pafupi. Vula nsapato zakozo, chifukwa malo waimapowo ngoyera.” Adapitirira kunena kuti, “Ine ndine Mulungu wa makolo ako, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, Mulungu wa Yakobe.” Pompo Mose adadziphimba kumaso chifukwa adaopa kupenya Mulungu. Kenaka Chauta adati, “Ndaona m'mene anthu anga akuzunzikira ku Ejipito. Ndamva kulira kwao kofuna chithandizo, chifukwa cha anthu amene akuŵapsinja. Ndikudziŵa bwino kuzunzika kwao. Ndabwera kuti ndiŵapulumutse kwa Aejipito ndi kuŵatulutsa m'dziko limenelo, kuti ndikaŵaloŵetse m'dziko lalikulu lachonde. Dziko limenelo ndi lamwanaalirenji. Amene akukhala m'dziko limenelo ndi Akanani, Ahiti, Aamori, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi. Ine ndamva ndithu kulira kwa Aisraele, ndipo ndaŵaonadi mazunzowo amene Aejipito akuŵapsinja nawo. Tsono iwe ndikukutuma kwa Farao kuti ukatulutse anthu anga Aisraele ku Ejipito.” Apo Mose adafunsa kuti, “Kodi ndine yani ine, kuti ndingapite kwa Farao ndi kukatulutsa Aisraele ku Ejipito?” Mulungu adamuyankha kuti, “Ine ndidzakhala nawe. Chitsimikizo chakuti ndakutuma ndine nachi: Utaŵatulutsa anthu anga ku Ejipito, mudzandipembedza pa phiri lomwe lino.” Mose adayankha kuti, “Tsono ine ndikapita kwa Aisraelewo kukaŵauza kuti Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu, iwowo akakandifunsa kuti, ‘Dzina lake ndani?’ Ndiye ineyo ndikaŵauze chiyani?” Mulungu adamuuza kuti, “Dzina langa ndine NDILIPO. Aisraelewo ukaŵauze kuti, NDILIPO wandituma kwa inu.” Ndipo Mulungu adamuuzanso Mose kuti, “Aisraele ukaŵauze kuti, Chauta, Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, Mulungu wa Yakobe, ndiye amene wandituma kwa inu. Tsono limeneli ndilo dzina langa mpaka muyaya. Limeneli ndilo dzina limene idzanditchula mibadwo yonse yam'tsogolo. Pita ukaŵasonkhanitse atsogoleri onse a Aisraele, ukaŵauze kuti, Chauta, Mulungu wa Abrahamu, Isaki ndi Yakobe, adandiwonekera; adandilamula kuti ndikuuzeni kuti wabwera kwa inu, ndipo zonse zimene akukuchitani Aejipito, waziwona. Mulungu watsimikiza kuti adzakutulutsani ku Ejipito kuno kumene mukuzunzika, ndipo adzakuloŵetsani m'dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi. Dzikolo ndi lamwanaalirenji.” Mulungu adapitirira kunena kuti, “Zimene ukaŵauzezo, adzamva. Ndiye mukapite kwa mfumu ya ku Ejipito, iwe ndi atsogoleri a Aisraelewo, ndipo mfumuyo mukaiwuze kuti, ‘Chauta, Mulungu wa Ahebri, adakumana nafe. Tsono tikukupemphani, mutilole kuti tipite ulendo wa masiku atatu ku chipululu, kuti tikapereke nsembe kwa Chauta, Mulungu wathu.’ Kudziŵa ndikudziŵa kuti mfumu ya ku Ejipitoyo sidzakulolani kuti mupite, mpaka nditaikakamiza kutero. Tsono Ine ndidzagwiritsa ntchito mphamvu zanga ndipo ndidzalanga Ejipito ndi zozizwitsa zomwe ndidzachite kumeneko. Zikadzachitika zimenezo, adzakulolani. Aejipito ndidzaŵafeŵetsa mtima pa anthu anga, kotero kuti pamene muzidzachoka, simudzapita chimanjamanja. Mkazi aliyense adzapempha Mwejipito woyandikana naye ndiponso amene amakhala naye m'nyumba, kuti ampatse zinthu zodzikongoletsera zasiliva ndi zagolide, ndiponso zovala. Zimenezi mudzaveka ana anu aamuna ndi aakazi, motero mudzaŵalanda zonse Aejipitowo.” Mose adayankha kuti, “Koma Aisraelewo sakandikhulupirira, kapena kumvera mau anga. Adzati, ‘Chauta sadakuwonekere.’ ” Chauta adafunsa Moseyo kuti, “Kodi nchiyani chili m'manja mwakocho?” Mose adayankha kuti, “Ndodo.” Chauta adamuuza kuti, “Taiponya pansi.” Mose ataiponya pansi ndodoyo, idasanduka njoka, iye nkuithaŵa njokayo. Apo Chauta adauza Mose uja kuti, “Igwire mchira.” Mose adaigwira, pompo idasandukanso ndodo m'manja mwakemo. Chauta adamuuza kuti, “Ukachite zimenezi, ndipo adzakhulupirira kuti Chauta, Mulungu wa makolo ao, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, Mulungu wa Yakobe, adakuwonekeradi.” Chauta adauzanso Mose kuti, “Tapisa dzanja lako m'malayamo.” Iye adapisadi. Koma potulutsa dzanjalo, linali lakhate, lotuŵa ngati ufa. Tsono Chauta adati, “Lipisenso m'malayamo dzanja lakolo.” Iye adalipisanso ndipo potulutsa, linali labwinobwino lopanda khate, koma lofanana ndi thupi lake lonse. Pamenepo Chauta adati, “Akakapanda kukukhulupirira, osasamala chizindikiro choyambacho, akakhulupirira ndithu chifukwa cha chizindikiro chachiŵiricho. Koma akakapanda kukhulupirira zizindikiro ziŵiri zonsezo, osafuna kumva zomwe ukaŵauzezo, ukatenge madzi a mu mtsinje wa Nailo, ukaŵathire pa nthaka youma. Madzi amenewo akasanduka magazi.” Mose adati, “Pepani Chauta, ndapota nanu, ine sindidziŵa kulankhula bwino chiyambire kale, kapena kuyambira paja mwayamba kulankhula nane mtumiki wanune. Lilime langa ndi lolemera, ndine wachibwibwi.” Apo Chauta adafunsa Mose kuti, “Kodi adapatsa munthu pakamwa ndani? Ndani amasandutsa munthu kuti akhale wosamva kapena wosalankhula, wopenya kapena wosapenya? Kodi si ndine Chauta amene ndimachita zimenezo? Tsono pita, Ine ndidzakuthandiza kulankhulako, ndipo zoti ukanene ndidzakuuza ndine.” Koma Mose adati, “Pepani Chauta, ndikukupemphani kuti mutume wina amene angathe kulankhula bwino.” Pompo Chauta adamkalipira Mose, namufunsa kuti, “Bwanji mbale wako Aroni, Mlevi uja? Ndikudziŵa kuti angathe kulankhula bwino kwambiri. Iyeyo akubwera kudzakumana nawe, ndipo adzakondwa kwambiri pokuwona. Udzalankhula naye iyeyo ndi kumuuza zoti akanene. Ndidzakuthandizani kulankhula nonse aŵirinu, ndipo ndidzakuuzaninso zoti mukachite. Iye azikalankhula kwa anthu m'malo mwako. Adzakhala wokulankhulira, ndipo iweyo udzakhala ngati Mulungu ndiwe kwa Aroni. Utenge ndodo ili m'manja mwakoyo, ukachite nayo zozizwitsa ndodo imeneyo.” Tsono Mose adabwerera kwa Yetero mpongozi wake uja, namuuza kuti, “Chonde mundilole kuti ndibwerere ku Ejipito kwa abale anga, kuti ndikaŵaone ngati ali moyo.” Yetero adauza Mose kuti, “Pitani ndi mtendere.” Chauta adauza Mose ku Midiyani kuja kuti, “Bwerera ku Ejipito tsopano popeza kuti onse aja ankafuna kukuphaŵa adamwalira.” Motero Mose adatenga mkazi wake ndi ana ake, naŵakweza pa bulu onsewo, ndipo adapita ku Ejipito, atatenga ndodo imene adampatsa Mulungu ija. Chauta adauzanso Mose kuti, “Pamene ukubwerera ku Ejipito, ukachite ndithu pamaso pa Farao zozizwitsa zonse zimene ndakuuza kuti ukachite. Koma ndidzamuumitsa mtima, ndipo sadzalola kuti anthu anga apite. Ndipo ukamuuze Farao kuti, Ine Chauta ndikuti Israele ali ngati mwana wanga wachisamba. Choncho ndikukuuza kuti umlole mwana wanga apite akandipembedze Ine. Tsono iweyo ukakana, Ine ndidzapha mwana wako wamwamuna wachisamba.” Pambuyo pake Chauta adakumana naye Mose pa njira pa malo a chigono, nafuna kumupha. Koma Zipora adatenga mwala wakuthwa, naumbala mwana wake, ndipo khungulo adalikhudzitsa m'miyendo mwa Mose. Kenaka Ziporayo adati, “Zoonadi, iwe ndiwe mkwati woomboledwa ndi magazi.” Choncho Chauta adamleka Mose osamupha. Ndiye pamene Zipora adanena kuti, “Ndiwe mkwati woomboledwa ndi magazi,” chifukwa cha kuumbalako. Chauta adauza Aroni kuti, “Pita ku chipululu kuti ukakumane ndi Mose.” Aroni adapitadi kukakumana naye ku phiri la Mulungu, namumpsompsona. Pamenepo Mose adafotokozera Aroni zonse zimene Chauta adaamuuza, pa nthaŵi imene ankamutuma. Adamuuzanso za zozizwitsa zonse zija zimene Chauta adamlamula kuti akachite. Motero Mose ndi Aroni adapita, nakasonkhanitsa atsogoleri onse a Aisraele. Aroni adafotokozera atsogoleriwo zonse zimene Chauta adaauza Mose, ndipo adachita zozizwitsa zonse zija anthuwo akupenya. Pamenepo Aisraele aja adakhulupiriradi zimenezo. Tsono atamva kuti Chauta adadzaŵayendera ndipo kuti adaona kuzunzika kwaoko, adaŵeramitsa mitu pansi napembedza. Pambuyo pake Mose ndi Aroni adapita kwa Farao nakamuuza kuti, “Naŵa mau a Chauta, Mulungu wa Aisraele, akunena kuti, ‘Uŵalole anthu anga apite ku chipululu, kuti akachite mwambo wachipembedzo wondilemekeza Ine.’ ” Farao adayankha kuti, “Kodi Chautayo ndani kuti ine nkumvera zimenezo ndi kuŵalola Aisraele kuti apite? Chautayo sindimdziŵa, ndipo sindidzalola konse kuti Aisraele apite.” Koma iwo adamuuza kuti, “Mulungu wa Ahebri adalankhula nafe. Chonde tiloleni kuti tipite ku chipululu ulendo wa masiku atatu, kuti tikapereke nsembe kwa Chauta, Mulungu wathu. Tikapanda kupita adzatipha ndi matenda kapena nkhondo.” Koma mfumu ya ku Ejipito ija idafunsa Mose ndi Aroni kuti, “Chifukwa chiyani mukuŵasiyitsa ntchito yao Aisraele? Chokani apa, bwererani ku ntchito yanu.” Farao adapitirira kuŵauza kuti, “Anthu ameneŵa akuchulukana kwambiri tsopano. Bwanji inu mufuna kuŵaletsa kugwira ntchito yao?” Motero pa tsiku limenelo Farao adalamula akuluakulu a thangata, pamodzi ndi akapitao achiisraele kuti, “Musaŵapatsenso udzu wa njerwa anthu ameneŵa, monga muja munkachitiramu. Alekeni azikamweta okha udzuwo. Koma chiŵerengero cha njerwa chikhale chonchija, monga momwe ankaumbira kale. Musaŵachepetsere ndi pang'ono pomwe, ngaulesi ameneŵa. Nchifukwa chake akulira nkumati, ‘Tiyeni tikapereke nsembe kwa Mulungu wathu.’ Muŵagwiritse ntchito yakalavulagaga anthu ameneŵa, kuti azitanganidwa ndi ntchito m'malo momangomvera zabodza.” Akuluakulu a thangata ndi akapitao Achiisraele adapita kukaŵauza anthu kuti, “Farao wanena kuti, ‘Sindidzakupatsaninso udzu. Muzidzimwetera nokha kulikonse komwe mungaupeze. Koma chiŵerengero cha njerwa ndi chonchija.’ ” Motero anthu aja adamwazikira m'dziko lonse la Ejipito kukafunafuna udzuwo. Akulu a Farao aja ogwiritsa ntchito, adafulumizitsa Aisraele naŵauza kuti, “Muziwumba chiŵerengero chonchija cha njerwa pa tsiku, monga munkachitira pamene ankakupatsani udzu.” Akuluakulu a thangata a Farao aja ankamenyanso akapitao Achiisraele amene adaŵaika kuti akhale omayang'anira ntchito, namaŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani lero simudaumbe chiŵerengero chonchija cha njerwa monga munkachitira kale?” Tsono akapitao achiisraele aja adapita kwa Farao kukadandaula kuti, “Pepani amfumu, kaya chifukwa chiyani mwatichita zotere ife atumiki anu? Udzu satipatsanso ife, bwana, komabe akutilamula kuti, ‘Kaziwumbani njerwa!’ Ndiponso akungotimenya. Anthu anu akulakwa.” Farao adaŵayankha anthuwo kuti, “Ndinu alesi inu, alesi zedi, nchifukwa chake mukuti, ‘Tiyeni tipite tikapereke nsembe kwa Chauta.’ Chokani apa, bwererani ku ntchito yanu. Udzu asakupatseni, koma chiŵerengero cha njerwa ndi chonchija ndithu basi.” Akapitao achiisraele aja adaona kuti alidi pa mavuto, ataŵauza kuti, “Muziwumba chiŵerengero chonchija cha njerwa tsiku ndi tsiku.” Tsono atachoka kwa Farao kuja, adakumana ndi Mose ndi Aroni amene ankaŵadikira, ndipo adaŵauza kuti, “Chauta aone mwachitazi, ndipo akuweruzeni inu poti Farao ndi nduna zake mwaŵasandutsa adani athu. Inuyo ndinu amene mwaika lupanga m'manja mwao kuti atiphe ife.” Choncho Mose adapemphera kwa Chauta nati, “Inu Chauta, chifukwa chiyani mukuzunza anthu anu? Nanga ine mudanditumiranji? Chipitire changa chija kwa Farao kukamuuza mau anu aja, wakhala akuzunzabe anthu anu. Ndipo Inu simudachitepo kanthu konse kuti muŵaombole anthu anu.” Chauta adauza Moseyo kuti, “Uwona tsopano zimene ndimchite Farao. Ndidzakakamiza Farao kuti atulutse anthu anga m'dziko lake. Ndithudi, adzaŵatulutsiratu m'dzikomo, chifukwa ndidzamkakamiza ndi dzanja langa lamphamvu. Zoonadi, dzanja langa lamphamvu lidzamuumiriza kuti aŵapirikitse.” Mulungu adalankhula ndi Mose namuuza kuti, “Ine ndine Chauta. Ndidaonekera Abrahamu, Isaki ndi Yakobe ngati Mulungu Mphambe, koma sindidaŵadziŵitse dzina langa kuti ndine Chauta. Ndidachita nawo chipangano ndi kuŵalonjeza kuti ndidzaŵapatsa dziko la Kanani, momwe adakhalamo kale ngati alendo. Tsopano ndamva kudandaula kwa Aisraele, amene ali mu ukapolo wa Aejipito, ndipo ndakumbukira chipangano changa. Tsono iwe ukaŵauze Aisraele mau anga oti, ‘Ine ndine Chauta. Ndidzakutulutsani mu ukapolo wa ntchito yakalavulagaga imene Aejipito akukukakamizani kuigwira. Ndidzakupulumutsani ndi dzanja langa lotambalitsa ndiponso pochita ntchito zamphamvu. Inu mudzakhala anthu anga, Ine ndidzakhala Mulungu wanu. Mudzazindikira kuti ndine Chauta, Mulungu wanu, amene ndidakupulumutsani ku ntchito yakalavulagaga imene Aejipito akukukakamizani kuigwira. Ndipo ndidzakufikitsani ku dziko limene ndidalumbira kuti ndidzapatsa Abrahamu, Isaki ndi Yakobe. Ndidzakupatsani dziko limenelo kuti likhale lanulanu. Ine ndine Chauta.’ ” Mose adauza Aisraele zimenezi, koma iwo sadamvere, chifukwa choti anali atataya kale mtima, pomakhala mu ukapolo wao mwankhalwe chotere. Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Pita kamuuze Farao, mfumu ya ku Ejipito, kuti aŵalole Aisraele kutuluka m'dziko mwake.” Koma Mose adauza Chauta kuti, “Ngati Aisraele enieniwo sandimvera ine, nanji Farao angandimvere bwanji? Inetu paja sindikhoza kulankhula bwino.” Koma Chauta adalamula Mose ndi Aroni kuti akauze Aisraele ndi Farao mfumu ya ku Ejipito, kuti Aisraelewo ayenera kutuluka m'dziko la Ejipito. Naŵa atsogoleri a mabanja a makolo ao. Ana a Rubeni, mwana wachisamba wa Israele, anali aŵa: Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karimi. Ameneŵa ndiwo a m'banja la Rubeni. Ana a Simeoni naŵa: Yemuwele, Yamini, Ohadi, Yakini, Zohari ndi Shaulo mwana wa kwa mkazi wa ku Kanani. Ameneŵa ndiwo a m'banja la Simeoni. Maina a ana a Levi pamodzi ndi zidzukulu zao naŵa: Geresoni, Kohati ndi Merari. Leviyo adakhala zaka 137 ali moyo. Ana a Geresoni naŵa: Libini ndi Simeyi pamodzi ndi mabanja ao. Ana a Kohati naŵa: Amuramu, Izihara, Hebroni ndi Uziyele. Kohati adakhala zaka 133 ali moyo. Ana a Merari naŵa: Mali ndi Musi. Ameneŵa ndiwo mabanja a Levi pamodzi ndi zidzukulu zao. Amuramu adakwatira mlongo wa bambo wake dzina lake Yokebede. Yokebedeyo adabala Aroni ndi Mose. Amuramu adakhala zaka 137 ali moyo. Ana a Izihara naŵa: Kora, Nefegi ndi Zikiri. Ana a Uziyele naŵa: Misaele, Elizafani ndi Sitiri. Aroni adakwatira Eliseba mwana wa Aminadabu, ndipo mlongo wake anali Nasoni. Eliseba adabala Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara. Ana a Kora naŵa: Asiri, Elikana ndi Abiyasafu. Ameneŵa ndiwo mabanja a Kora. Eleazara mwana wa Aroni adakwatira mmodzi mwa ana a Putiyele, amene adamubalira Finehasi. Ameneŵa ndiwo atsogoleri a mabanja a Alevi malinga ndi mafuko ao. Mose ndi Aroni ndi omwe aja amene Chauta adaŵauza kuti, “Atulutseni Aisraele m'dziko la Ejipito mwa magulumagulu.” Ameneŵa ndiwo ankauza Farao mfumu ya ku Ejipito kuti atulutse Aisraele ku Ejipito. Pamene Chauta adalankhula ndi Mose ku dziko la Ejipito, adati “Ine ndine Chauta. Ukamuuze Farao, mfumu ya ku Ejipito, zonse zimene ndikuuze.” Koma Mose adauza Chauta kuti, “Inu mukudziŵa kuti paja ndine wosakhoza kulankhula, nanga Faraoyo adzandimvera bwanji?” Chauta adauza Mose kuti, “Taona, ndidzakusandutsa kuti ukhale ngati Mulungu kwa Farao, ndipo mbale wako Aroni ndiye adzakhale ngati mneneri wako. Zonse zimene ndakulamulazi ukazinene, ndipo iye ndiye akauze Farao kuti aŵalole Aisraele kutuluka m'dziko mwake. Komatu ndidzamuumitsa mtima, ndipo ngakhale ndidzachite zozizwitsa zambiri ndi zodabwitsa ku Ejipito, Faraoyo sadzakumverani. Pamenepo ndidzakantha dzikolo, ndipo pochita ntchito zamphamvu, ndidzatsogolera magulu anga, anthu anga Aisraele, kuŵatulutsa ku Ejipito. Apo Aejipito adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndikadzaŵakantha ndi dzanja langa ndi kutulutsa Aisraele m'dziko mwaomo.” Ndipo Mose ndi Aroni adachitadi zomwe Chauta adaŵalamulazo. Pamenepo nkuti Mose ali wa zaka 80 ndipo Aroni wa zaka 83, pa nthaŵi imene ankalankhula ndi Farao. Tsono Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti, “Ngati Farao akulamulani kuti, ‘Chitani chozizwitsa kuti tikukhulupirireni,’ iwe Mose ukauze Aroni kuti, ‘Tenga ndodo yako, iponye pansi pamaso pa Farao kuti isanduke njoka.’ ” Choncho Mose ndi Aroni adapita kwa Farao nakachita monga momwe Chauta adaŵalamulira. Aroni adaponya pansi ndodo yake ija pamaso pa Farao ndi nduna zake, ndipo idasanduka njoka. Zitatero Farao adaitana anthu ake anzeru ndi amatsenga, ndipo iwowo adachitanso zomwezo mwa matsenga ao. Adaponyanso pansi ndodo zao, ndipo zidasanduka njoka. Koma ndodo ya Aroni ija idameza ndodo zaozo. Farao adaumabe mtima, ndipo sadasamale zimene ankamuuzazo monga momwe Chauta adaanenera muja. Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Farao ndi wokanika kwambiri, akukana kulola anthu anga kuti apite. Upite m'maŵa ukakumane naye pamene akupita ku mtsinje wa Nailo. Ukamdikire pambali pa mtsinjewo. Tsono utenge ndodo ija idaasanduka njokayi. Ukamuuze Farao kuti Chauta, Mulungu wa Ahebri, wandituma kwa inu kuti ndikuuzeni mau aŵa: ‘Uŵalole anthu anga apite, akandipembedze ku chipululu. Koma mpaka tsopano lino sudandimverebe.’ Zimene Chauta akunena ndi izi, akuti ‘Poona zimene ndichite, udzadziŵa kuti Ine ndinedi Chauta. Taona, ndidzamenya madzi a mu mtsinjewu ndi ndodo ili m'manja mwangayi, ndipo madzi onseŵa adzasanduka magazi. Nsomba zonse zidzafa, ndipo madziwo adzanunkha, kotere kuti Aejipito sadzafunanso kumwa madzi a mu mtsinje umenewu.’ ” Chauta adalamulanso Mose kuti, “Uza Aroni kuti, ‘Tenga ndodo yako, uilozetse ku madzi onse mu Ejipito muno, monga mitsinje, ngalande ndiponso zithaphwi ndi maiŵe omwe. Madziwo adzasanduka magazi, ndipo m'dziko monsemo mudzakhala magazi okhaokha, ngakhale m'zotungira madzi zomwe, zamitengo ndi zamiyala.’ ” Motero Mose ndi Aroni adachita monga momwe Chauta adaŵalamulira. Aroni adasamula ndodo yake namenya madzi amumtsinje pamaso pa Farao ndi nduna zake, ndipo madzi onsewo adasanduka magazi. Nsomba zonse zamumtsinjemo zidafa, ndipo kununkha kwake kwa madziwo kunali kwakuti Aejipito sadathenso kuŵamwa. Ndipo munali magazi okhaokha m'dziko lonse la Ejipito. Tsono amatsenga a ku Ejipito aja nawonso adachita zomwezo mwa matsenga ao, ndipo Farao adakhalabe wokanika. Sadamvere zimene ankanena Mose ndi Aroni monga momwe Chauta adaanenera muja. Pompo Farao adapotoloka, napita kunyumba kwake osalabadanso zimenezo. Aejipito onse adayamba kukumba m'mbali mwa mtsinje wa Nailo kuti apeze madzi akumwa, chifukwa sankathanso kumwa madzi a mu mtsinjewo. Padapita masiku asanu ndi aŵiri, Chauta ataipitsa mtsinje uja. Pambuyo pake Chauta adalamula Mose kuti, “Pita kwa Farao ukamuuze kuti, Chauta akuti, ‘Uŵalole anthu anga apite akandipembedze. Ukakana kuŵalola, dziko lako lonse ndidzalilanga polidzaza ndi achule. Mtsinje uja udzakhala wodzaza ndi achule. Adzachokera mumtsinjemo namakaloŵa m'chipinda mwako mogona, pabedi pako, m'nyumba za nduna zako ndi za anthu ako, m'malo onse ophikira ndi mophikira buledi momwe. Azidzakulumphira iwe, pamodzi ndi anthu ako, ndi nduna zako zonse.’ ” Chauta adauzanso Mose kuti, “Uza Aroni kuti, ‘Uloze ndodo yako ku mitsinje, ku ngalande ndi ku zithaphwi ndipo pakhale achule pa dziko lonse la Aejipito.’ ” Choncho Aroni adaloza ndodo yake pa madzi, ndipo achule adatuluka, nadzaza dziko lonselo. Koma amatsenga aja nawonso adapanga ao achule ndipo adayamba kukwera pa mtunda. Pomwepo Farao adaitana Mose ndi Aroni naŵauza kuti, “Pempherani kwa Chauta kuti achuleŵa andichoke ine ndi anthu angaŵa, ndipo ndidzaŵalola anthu anu kuti apite kukapereka nsembe kwa Chauta.” Tsono Mose adauza Farao kuti, “Chabwino, mungondiwuza nthaŵi yoti ndikupempherereni inu, nduna zanu ndi anthu anu omwe, kuti achuleŵa akuchokeni, achokenso m'nyumba mwanu, ndipo kuti akakhale mumtsinje mokha.” Farao adati, “Maŵa.” Apo Mose adati, “Zidzachitika monga momwe mwaneneramu, ndipo mudzadziŵa kuti palibe Mulungu wina wofanafana ndi Chauta, Mulungu wathu. Achulewo adzakuchokani, adzachokanso m'nyumba zanu, m'nyumba za nduna zanu, ndipo azidzangokhala mumtsinje mokha.” Pamenepo Mose ndi Aroni adachoka kwa Farao kuja, ndipo adakapempha Chauta kuti achotse achule amene adaatumiza kwa Farao aja. Tsono Chauta adachitadi monga momwe Mose adapemphera. Motero achule onse aja amene adaali m'nyumba, pa bwalo ndi m'minda momwe, adafa. Aejipito aja adaŵaunjika achulewo milumilu, ndipo dziko lonse lidadzaza ndi chivunde chokhachokha. Farao ataona kuti zinthu zayamba kukhala bwino, adaumitsa mtima wake, ndipo sadafunenso kumvera Mose ndi Aroni monga momwe Chauta adaanenera muja. Pamenepo Chauta adalamula Mose kuti, “Uza Aroni asamule ndodo yake ndipo amenye nthaka, motero fumbi lonse lidzasanduka nthata m'dziko lonse la Ejipito.” Iwowo adachitadi momwemo. Aroni adasamula ndodo yake ija namenya nthaka. Tsono fumbi lonse lidasanduka nthata, ndipo zidabalalikira pa anthu ndi pa nyama zomwe. Motero fumbi lonse la ku Ejipito lidangokhala nthata zokhazokha. Amatsenga aja adayesanso momwemo mwa matsenga ao kuti apange zao nthata, koma adalephera. Ndipo nthatazo zidabalalikira pa anthu ndi nyama zomwe. Tsono amatsenga aja adauza Farao kuti, “Zimenezi wachita ndi Mulungu ndithu.” Koma Farao adakhala wokanikabe, ndipo sadamvere zimene Mose ndi Aroni ankanena monga momwe Chauta adaanenera muja. Apo Chauta adauza Mose kuti “Maŵa m'maŵa ndithu, upite ukakumane ndi Farao pamene akupita ku mtsinje, ukamuuze kuti, ‘Chauta akunena kuti uŵalole anthu anga apite, akandipembedze Ine. Ukapanda kulola anthu anga kuti apite, ndidzatumiza mizaza pa iwe, nduna zako, anthu ako ndi m'nyumba mwako. M'nyumba zonse za Aejipito, ngakhalenso pa nthaka yonse imene akukhalapo, padzakhala mizaza yokhayokha. Pa tsiku limenelo ndidzapatula dziko la Goseni lokhalamo anthu anga, mwakuti lokhalo lidzakhala lopanda mizaza, kuti iweyo udziŵe kuti Ine ndine Chauta ndipo kuti ndikulamulira pa dziko lapansi. Ndidzasiyanitsa ndithu pakati pa anthu anga ndi anthu ako. Chozizwitsa chimenechi chichitika maŵali.’ ” Choncho Chauta adachitadi zimenezi, ndipo magulu a mizaza adaloŵa m'nyumba ya Farao, m'nyumba za nduna zake, ndiponso m'dziko lonse la Ejipito. Dziko lonselo lidaipiratu ndi mizazayo. Tsono Farao adaitana Mose ndi Aroni naŵauza kuti, “Pitani mukapereke nsembe kwa Mulungu wanu m'dziko mommuno.” Koma Mose adayankha kuti, “Sikungakhale bwino konse kuchita zimenezo, chifukwa Aejipito zidzaŵaipira nsembe zimene timapereka kwa Chauta, Mulungu wathu. Tikadzapereka nsembe zimene Aejipito zimaŵanyansa m'maso mwao, kodi iwo sadzatiponya miyala mpaka kutipha? Tiyenera kuyenda ulendo wa masiku atatu m'chipululu, kuti tikapereke nsembe kwa Chauta, Mulungu wathu, monga adatilamulira.” Farao adati, “Ndidzakulolani kuti mupite mukapereke nsembe kwa Chauta, Mulungu wanu, ku chipululu, koma musapite kutali kwambiri. Tsono mundipempherere.” Apo Mose adati, “Malinga ndikachoka pano, ndikukapempha kwa Chauta, ndipo maŵa mizaza ikuchokani inu, nduna zanu ndiponso anthu anu. Koma musatinyengenso ndi kuŵaletsa anthu kupita kuti akapereke nsembe kwa Chauta.” Mose atachoka kwa Faraoko, adakapemphera kwa Chauta. Motero Chauta adachitadi monga momwe Mose adapemphera. Pomwepo mizaza idamchoka Farao ndi nduna zake ndi anthu ake omwe. Sudatsalepo ndi umodzi omwe. Koma ngakhale pa nthaŵi imeneyinso, Farao adakhala wokanikabe, ndipo sadalole kuti Aisraele apite. Pambuyo pake Chauta adalamula Mose kuti, “Pita kwa Farao ukamuuze kuti, ‘Chauta, Mulungu wa Ahebri, akunena kuti uŵalole anthu anga apite akandipembedze. Koma ukakananso kuŵalola kuti apite, ndi kuŵaletsa ndithu, dzanja la Chauta lidzakulanga ndi mliri woopsa pa zoŵeta zako monga akavalo, abulu, ngamira, ng'ombe, nkhosa ndi mbuzi zomwe. Ndidzasiyanitsa pakati pa zoŵeta za Aisraele ndi za Aejipito. Motero palibe choŵeta nchimodzi chomwe cha Aisraele chimene chidzafe. Chauta waika nthaŵi, ndipo akunena kuti zimenezi azichita maŵa.’ ” Tsono m'maŵa mwake Chauta adachitadi monga momwe adanenera, ndipo zoŵeta zonse za Aejipito zidafa. Koma panalibe choŵeta nchimodzi chomwe cha Aisraele chimene chidafapo. Ndipo Farao atafunsitsa zimene zidaachitikazo, adamva kuti palibe ndi chiŵeto nchimodzi chomwe cha Aisraele chimene chidafapo. Komabe Farao adakhala wokanika ndithu, ndipo sadalole konse kuti anthuwo apite. Pamenepo Chauta adalamula Mose ndi Aroni kuti, “Tapaniko phulusa lapamoto. Tsono Mose awaze phulusalo kumwamba pamaso pa Farao. Phulusalo lidzaulukira m'dziko lonse la Ejipito ngati fumbi. Ndipo konse kumene lidzaulukireko, kudzabuka zithupsa zomaphulika ndi kusanduka zilonda pa anthu ndi pa nyama zomwe.” Choncho Mose adatapa phulusalo pa moto ndipo adakaimirira pamaso pa Farao. Adawaza phulusalo kumwamba, ndipo padabuka zithupsa zimene zidaphulika ndi kusanduka zilonda pa anthu ndi pa nyama zomwe. Amatsenga aja sadathenso kufika pamaso pa Mose chifukwa iwonso anali ndi zithupsa zokhazokha, monga Aejipito onse. Koma Mulungu adamuumitsa mtima Farao, ndipo Faraoyo sadaŵalole anthuwo kuti apite monga momwe Chauta adaauzira Mose muja. Apo Chauta adauza Mose kuti, “Maŵa m'mamaŵa upite ukakumane ndi Farao, ukamuuze kuti, ‘Chauta, Mulungu wa Ahebri, akunena kuti uŵalole anthu anga kuti apite, akandipembedze. Tsopano ndikuti ndigwetsere miliri yanga yonse pa iwe, pa nduna zako, ndi pa anthu ako, ndipo udzadziŵa kuti palibe wina aliyense wofanafana ndi Ine pa dziko lonse lapansi. Ndikadasamula dzanja langa kuti ndikumenye iwe pamodzi ndi anthu ako, bwenzi tsopano nonsenu mutatha. Koma ndakusungani ndi moyo kuti muwone mphamvu zanga, kuti mbiri yanga iwande pa dziko lonse lapansi. Koma ukunyozabe anthu anga, osafuna kuŵalola kuti apite. Imvani tsono, nthaŵi yomwe ino maŵa, ndidzagwetsa matalala amphamvu amene sanagwepo nkale lonse mu Ejipito muno chiyambire cha dziko lino. Tsopano lamula kuti zoŵeta zanu zonse zikhale m'khola pamodzi ndi zonse zimene muli nazo. Matalala adzagwa pa anthu ndi pa nyama zonse zongoyenda pa bwalo, chifukwa chosaziloŵetsa m'khola, ndipo zonsezo zidzafa.’ ” Nduna zina za Farao zidachita mantha chifukwa cha mau amene adanena Chauta, ndipo zidatsekera akapolo ao m'nyumba pamodzi ndi zoŵeta zao zomwe. Komabe ena sadasamaleko zimene Chauta adanenazo, ndipo adangosiya panja akapolo ao pamodzi ndi zoŵeta zomwe. Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Kweza dzanja lako kumwamba, ndipo matalala adzagwa pa anthu, pa nyama, ndi pa zomera zonse zam'minda, m'dziko lonse la Ejipito.” Mose adakweza ndodo yake kumwamba. Pompo Chauta adatumiza mabingu ndi matalala, ndipo mphezi zidaomba pa nthaka. Chauta adagwetsa matalala pa dziko la Ejipito. Ndipo panali mvula yamatalala ndi mphezi zong'anima kwambiri. Matalala ake anali oopsa kwambiri, kotero kuti chiyambire pamene Aejipito adasanduka mtundu wa anthu oima paokha, matalala otere sadagwepo. Matalalawo adaononga zonse zokhala panja m'dziko lonse la Ejipito, anthu onse pamodzi ndi nyama zomwe. Adaononganso zomera zonse zam'minda ndi kukadzulanso mitengo yonse. Dziko la Goseni lokha, kumene kunkakhala Aisraele, matalalawo sadagweko mpang'ono pomwe. Pamenepo Farao adaitana Mose ndi Aroni naŵauza kuti, “Zoonadi, ndachimwa ndithu tsopano. Chauta ndi wolungama, koma ineyo pamodzi ndi anthu anga, tonse ndife ochimwa. Pemphera kwa Chauta kuti aŵaletse mabingu ndi matalalaŵa ndipo ndidzakulolani kuti mupite. Simudzakhalanso kuno ai.” Mose adamuuza kuti, “Ndikangotuluka mumzinda muno, ndikweza manja anga kwa Chauta. Tsono mabingu ndi matalala aleka, kuti inuyo mudziŵe kuti dziko lonse lapansi ndi la Chauta. Komabe ndikudziŵa kuti inu ndi nduna zanu simukuwopa Chauta.” Ndipo thonje lidaonongeka pamodzi ndi barele yemwe, chifukwa choti bareleyo anali atacha, ndipo thonjelo linali ndi nkhunje. Koma tirigu ndi rayi sizidaonongeke, chifukwa zimenezi amabzala mochedwa. Mose adachoka kwa Farao kuja, natuluka mumzindamo. Ndipo adakweza manja ake kumwamba, napemphera kwa Chauta. Tsono mabingu aja ndi matalala adaleka, ndipo mvula idakata. Farao ataona kuti mvula, matalala ndi mabingu, zonsezo zaleka, adakhala wokanikabe, nauma ndithu mtima iyeyo ndi nduna zake zija. Adakhala wokanika kwambiri, ndipo sadalole kuti Aisraele apite monga momwe Chauta adaauzira Mose muja. Chauta adauza Mose kuti, “Upite kwa Farao. Ndamuumitsa mtima iyeyo ndi nduna zake, kuti ndichite zozizwitsa zonsezi pakati pao. Ndipo inu, mudzaŵauze ana anu ndi zidzukulu zanu za m'mene ndidapusitsira Aejipito, pamene ndinkachita zozizwitsa pakati pao. Motero nonsenu mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.” Mose ndi Aroni adapita kwa Farao kukamuuza kuti, “Chauta, Mulungu wa Ahebri, akufunsa kuti, ‘Kodi udzakanabe kundigonjera mpaka liti? Uŵalole anthu anga kuti apite, akandipembedze. Ukakanabe kuŵalola kuti apite, ndikugwetsera dzombe maŵa m'dziko mwako. Nthaka yonse idzaphimbidwa ndi dzombelo, ndipo nthakayo sidzaoneka konse. Lidzadya zonse zomwe sizidaonongeke ndi matalala aja. Lidzadya mitengo yako yonse. Ndipo nyumba zako, nyumba za nduna zako ndi za anthu ako, zonse zidzakhala zodzaza ndi dzombe lokhalokha, chinthu chimene atate anu kapenanso makolo anu sadachiwone chibadwire chao.’ ” Tsono Mose adapotoloka nachoka kwa Farao kuja. Nduna za Farao zidafunsa Faraoyo kuti, “Kodi munthu ameneyu adzaleka liti kutivuta chotere? Aloleni anthuwo kuti apite, akapembedze Chauta, Mulungu wao. Kodi simukuwona kuti dziko la Ejipito latheratu kuwonongeka tsopano?” Motero Farao adaitananso Mose ndi Aroni naŵauza kuti, “Pitani mukapembedze Chauta, Mulungu wanu. Koma tsono apite ndani?” Mose adayankha kuti, “Tidzapita tonse ndi ana athu, pamodzi ndi nkhalamba zathu zomwe. Tidzapita ndi ana aamuna, ana aakazi, nkhosa zathu ndi mbuzi zomwe. Tidzatenganso ndi ng'ombe zomwe, chifukwa choti tikachita mwambo wachipembedzo wolemekeza Chauta.” Choncho Farao adaŵauza kuti, “Chauta akhale nanu ngati ine ndikulolani kuti mutenge akazi anu ndi ana anu. Nchodziŵikiratu kuti inu mukufuna kudzetsa mavuto. Ai! Inu, amuna nokhanu, ndiye mupite mukapembedze Chauta, popeza kuti ndi zimene mukufuna.” Atangomveka mau ameneŵa, Mose ndi Aroni adapirikitsidwa pamaso pa Farao. Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Tambalitsa dzanja lako pa dziko la Ejipito kuti dzombe libwere, ndipo lidzadye zomera zonse zimene matalala aja adasiya.” Choncho Mose adakweza ndodo yake kumwamba, ndipo Chauta adautsa mphepo yakuvuma kuti iwombe pa dziko usana ndi usiku womwe. Pamene kunkacha, nkuti ponseponse pali dzombe lokhalokha. Lidangophimba dziko lonse, ndipo lidakhazikika m'dzikomo. Kuchuluka kwake kwa dzombelo kunali kwakuti nkale lonse dzombe lotero silidaonekepo, ndipo silidzaonekanso. Lidangophimba nthaka yonse, ndipo nthakayo idada kuti bii chifukwa cha dzombelo. Lidadya kalikonse komera pa nthaka, pamodzi ndi zipatso zam'mitengo zimene matalala adasiyako. Palibe chachiŵisi chilichonse chimene chidatsalako pa mtengo kapena pa chomera chilichonse m'dziko lonse la Ejipito. Ndipo Farao adaitana Mose ndi Aroni mofulumira naŵauza kuti, “Ndachimwira Chauta, Mulungu wanu, ndipo ndachimwiranso inu. Koma pepani tsopano, khululukireni pa nthaŵi ino yokha, mupemphe kwa Chauta, Mulungu wanu, kuti andichotsere chilango choopsachi.” Mose adachoka kwa Farao kuja, nakapemphera kwa Chauta. Chauta adasintha mphepoyo kuti ikhale mphepo yamkuntho yakuzambwe, ndipo idapirikitsira dzombelo ku Nyanja Yofiira. Palibe dzombe ndi limodzi lomwe limene lidatsalako ku Ejipito kuja. Koma Chauta adamuumitsabe mtima Farao, ndipo sadaŵalole Aisraele kuti apite. Pambuyo pake Chauta adauza Mose kuti, “Kweza dzanja lako kumwamba kuti pagwe mdima wandiweyani pa dziko lonse la Ejipito.” Mose adakweza dzanja lake kumwamba, ndipo pa masiku atatu, mudagwa mdima wandiweyani m'dziko lonse. Aejipitowo sankathanso kuwonana, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adachoka pakhomo pake masiku atatu onsewo. Koma Aisraele okha ankakhala koŵala ndithu kuja ankakhalaku. Apo Farao adaitana Mose namuuza kuti, “Pitani mukapembedze Chauta. Mupite nawonso akazi anu ndi ana anu omwe. Koma nkhosa zanu, mbuzi zanu ndi ng'ombe zomwe, zidzasungidwa konkuno.” Mose adati, “Tsonotu muyenera kutipatsa ndinu zokaperekera nsembe zopsereza kwa Chauta, Mulungu wathu. Koma iyai, zoŵeta zathu zidzapita nafe limodzi ndipo sipadzatsala choŵeta nchimodzi chomwe kuno. Tiyenera kukasankha zoŵeta zokapembedzera nazo Chauta, Mulungu wathu. Mpaka tikafike kumeneko, sitingadziŵe zoyenera kuzigwiritsa ntchito popembedza Chauta.” Koma Chauta adaumitsa Farao mtima, ndipo sadalole kuti anthuwo apite. Farao adauza Mose kuti, “Choka apa. Chenjera, ndipo usafikenso pamaso panga, chifukwa tsiku lomwe ndidzakuwonelo, udzaphedwa ndithu.” Mose adayankha kuti, “Monga momwe mwaneneramu, ine sindidzakuwonaninso.” Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Tsopano ndimlanga kamodzi kokha Farao, pamodzi ndi Aejipito onse. Pambuyo pa chilango chimenechi, adzakulolani kuti muchoke. Zoonadi, akadzakulolani kuti muchoke, adzachita chokupirikitsani kuno. Tsopano lankhula ndi anthu, ndipo uuze mwamuna aliyense ndi mkazi aliyense, kuti apemphe zodzikongoletsera zasiliva ndi zagolide kwa Mwejipito aliyense woyandikana naye.” Ndipo Chauta adafeŵetsa Aejipito kuti akomere Aisraele mtima. Chinanso nkuti Mose anali wotchuka kwambiri m'dziko la Ejipito, pamaso pa nduna za Farao ndiponso pamaso pa anthu onse. Tsono Mose adauza Farao kuti, “Chauta akunena kuti, ‘Ndiyenda pakati pa Aejipito pakati pa usiku, ndipo mwana aliyense wachisamba adzaphedwa mu Ejipito monse muno. Kuyambira mwana wachisamba wa Farao, amene ali woyenera kuloŵa ufumu, adzaphedwa, mpaka mwana wachisamba wa mdzakazi amene akupera pa mphero. Mwana woyamba kubadwa wa zoŵeta adzafanso. M'dziko lonse la Ejipito mudzakhala maliro okhaokha amene sadaonekepo nkale lonse, ndipo sadzaonekanso. Koma pakati pa Aisraele, ndi galu yemwe sadzauwa munthu kapena choŵeta chilichonse, kuti mudziŵe kuti Chauta amasiyanitsa Aejipito ndi Aisraele. Nduna zanu zonse zidzabwera kwa ine kudzandigwadira, zidzati, “Chokani inu pamodzi ndi anthu anu onse!” Tsono pambuyo pake, ndidzachoka.’ ” Mose adachoka kwa Farao kuja mokwiya kwambiri. Chauta adauza Mose kuti, “Farao sadzakumvera iwe, kuti pakutero, Ine ndichite zozizwitsa m'dziko la Ejipito.” Motero Mose ndi Aroni adachita zozizwitsa zonsezi pamaso pa Farao. Koma Chauta adamuumitsa mtima Faraoyo, ndipo Aisraelewo sadaŵalole kuti achoke m'dziko mwake. Chauta adalankhula kwa Mose ndi Aroni m'dziko lija la Ejipito kuti, “Mwezi uno udzakhala mwezi wanu woyambira chaka. Mulengeze kwa khamu lonse la Aisraele kuti pa tsiku lakhumi la mwezi uno, munthu aliyense adzasankhulire banja lake mwanawankhosa mmodzi. Banja lililonse lidzatenge mwanawankhosa mmodzi. Banja likachepa, kuti silingathe kudya nyama yonseyo, mabanja aŵiri oyandikana aphatikizane pamodzi, monga momwe aliri anthu, tsono onsewo adyere limodzi. Mulinganiziretu chiŵerengero cha anthu odya nyamayo, modziŵa m'mene munthu mmodzi angadyere. Mwanawankhosa wake adzakhale wopanda chilema, wamphongo, wa chaka chimodzi. Mungathe kusankhulanso mwanawambuzi. Mumsunge mpaka tsiku la 14 la mwezi, pamene khamu lonse la Aisraele lidzaphe nyama zaozo madzulo ndithu. Tsono adzatengeko magazi a nyamayo ndi kuwaza pa mphuthu ziŵiri za chitsekozo, ndi pamwamba pa chitseko cha nyumba m'mene akadyeremo nyamayo. Nyamayo adzaiwotche usiku womwewo, ndipo adzaidye ndi buledi wosafufumitsa ndiponso ndi ndiwo zoŵaŵa zamasamba. Musaidye yaiŵisi kapena yophika, koma muwotche yonse pamodzi ndi mutu wake womwe, miyendo ndi zonse zam'kati. Musasiyeko nyama ina mpaka m'maŵa, motero ina ikatsalako, muitenthe. Kudya kwake, muzikadya motere: Mudzavale zaulendo, nsapato zanu zili kuphazi, ndodo zili kumanja. Mudzadye mofulumira. Limeneli ndilo tsiku la Paska ya Chauta. Usiku umenewo, Ine ndidzapita m'dziko la Ejipito ndipo m'dziko lonselo ndidzapha ana onse oyamba kubadwa, a anthu ndi a nyama omwe. Ndidzalanga milungu yonse ya Ejipito. Ine ndine Chauta. Magaziwo adzakhala chizindikiro pa nyumba zimene mumakhalamo. Ndikadzangoona magaziwo, ndidzakupitirirani inuyo, ndipo mliri wosakaza sudzakugwerani, pamene ndidzakanthe dziko la Ejipito. “Tsiku limeneli muzidzalisunga. Tsiku limeneli muzidzalikumbukira, ndipo muzidzachita chikondwerero, kupembedza Chauta. Mibadwo yonse izidzakumbukira tsikuli, kuti likhale lamulo lamuyaya, lakuti muzidzachita chikondwerero pa tsiku limenelo.” Tsono Chauta adati, “Muzidzadya buledi wosafufumitsa pa masiku asanu ndi aŵiri. Pa tsiku loyamba muzidzachotsa zotupitsira buledi m'nyumba zanu zonse, chifukwa pa masiku asanu ndi aŵiri aliyense wodya buledi wofufumitsa adzachotsedwa pakati pa Aisraele. Pa tsiku loyamba, ndi pa tsiku lachisanu ndi chiŵirilo, muzidzachita msonkhano wachipembedzo. Musadzagwire ntchito pa masiku amenewo, koma chakudya chokha choti aliyense adye, mudzatha kukonza. Chikondwerero chimenechi cha buledi wosafufumitsa, mudzachisunge ndithu, chifukwa pa tsiku limeneli mpamene ndidzatulutse magulu anu onse kuchoka m'dziko la Ejipito. Tsono muzidzasunga tsiku limeneli pa mibadwo yanu yonse, ngati lamulo lamuyaya. Muzidzadya buledi wosafufumitsa kuyambira madzulo a tsiku la 14 la mwezi woyamba, mpaka madzulo a tsiku la 21 mwezi womwewo. Pa masiku asanu ndi aŵiri onsewo, m'nyumba mwanu musadzapezeke chofufumitsira buledi, chifukwa wina aliyense akadzadya chakudya chofufumitsa, adzachotsedwa pa mtundu wa Aisraele, mlendo ngakhale mbadwa yomwe. Musadye chilichonse chofufumitsa, ndipo ku nyumba zanu zonse muzidzangodya buledi wosafufumitsa.” Ndipo Mose adaitana atsogoleri onse a Aisraele, naŵauza kuti, “Pitani kasankhuleni mwanawankhosa woyenera pa banja lililonse, ndipo muphe nyama ya Paskayo. Mutenge nthambi ya kachitsamba ka hisope, muiviike m'magazi amene mwaŵathira m'mbale. Tsono muwaze magaziwo pa mphuthu ziŵiri za chitsekozo ndi pamwamba pa chitseko. Wina aliyense asatuluke m'nyumba mwake mpaka m'maŵa. Chauta adzapita m'dziko lonse la Ejipito, ndi kumapha Aejipito. Azidzati akaona magaziwo pamwamba pa chitseko ndi pa mphuthu ziŵiri za chitsekozo, azidzapitirira khomolo ndipo sadzamulola mngelo wake woononga kuti aloŵe m'nyumba mwanu kuti akupheni. Muziŵamvera malamulo ameneŵa inuyo ndi ana anu mpaka muyaya. Ndipo mukadzaloŵa m'dziko limene Chauta akukupatsanilo, monga momwe adalonjezera, muzidzasunga mwambo umenewu. Ana anu azidzakufunsani kuti, ‘Kodi mwambo umenewu umatanthauza chiyani?’ Pamenepo inu muzidzayankha kuti, ‘Ndi nsembe ya Paska ya Chauta, chifukwa chakuti adapitirira nyumba za Aisraele ku Ejipito; pamene ankapha Aejipito, nyumba zathu adazisiya.’ ” Atamva zimenezi, anthu adaŵerama pansi, napembedza. Aisraele adapita, ndipo adamvera zimenezo. Adachitadi zonse zimene Chauta adalamula Mose ndi Aroni. Pakati pa usiku, Chauta adapha ana onse achisamba m'dziko la Ejipito. Adayambira mwana wachisamba wa Farao amene ankayembekezeka kuloŵa ufumu wake, mpaka ana a akaidi a m'nyumba zamdima za m'ndende. Ana onse oyamba kubadwa a nyama adaphedwanso ndithu. Farao ndi nduna zake zonse, pamodzi ndi Aejipito onse, adadzuka pakati pa usiku, ndipo m'dziko lonse la Ejipito munali maliro okhaokha, chifukwa panalibe banja lopanda mwana wakufa. Usiku womwewo Farao adaitana Mose ndi Aroni, ndipo adaŵalamula kuti, “Inu pamodzi ndi Aisraele onse, fulumirani, mutuluke. Asiyeni anthu anga, pitani mukapembedze Chauta monga momwe mudanenera. Mutenge nkhosa zanu, mbuzi zanu ndi ng'ombe zanu zomwe, monga momwe mudanenera, ndipo muchoke. Mukapemphere kuti nanenso andidalitseko.” Aejipito adafulumizitsa anthu kuti achoke m'dzikomo, namanena kuti, “Tifatu tonsefe.” Motero anthuwo adanyamula pa mapewa ao ufa wa buledi wokandiratu asanathire chofufumitsira, pamodzi ndi mbale zokandiramo buledi zili zokulunga m'nsalu. Ndiponso Aisraele anali atachita monga momwe Mose adaaŵauzira. Adaapempha kwa Aejipitowo zodzikongoletsera zasiliva ndi zagolide, ndiponso zovala. Chauta adasandutsa Aejipito aja kuti akhale okoma mtima, ndipo anthuwo adapatsa Aisraele zonse zimene ankapempha. Motero Aisraele adalandako chuma cha Aejipito aja. Tsono Aisraele adanyamuka ulendo kuchoka ku Ramsesi kupita ku Sukoti. Anthu aamuna analipo zikwi 600, osaŵerenga akazi ndi ana. Panalinso gulu lalikulu la anthu ena, ndiponso nkhosa, mbuzi pamodzi ndi ng'ombe zomwe. Adaphika mitanda ya buledi wosafufumitsa wa ufa wokandiratu, yomwe adachoka nayo ku Ejipito kuja. Ufa wabuledi wokandiratuwo unali wosathira chofufumitsira chifukwa anali atapirikitsidwa mwadzidzidzi ku Ejipito kuja. Panalibe nthaŵi yophikira chakudya chao cha kamba. Aisraele adakhalako zaka 430 ku Ejipito kuja. Pa tsiku lomwe zaka 430 zinkatha, magulu onse a Chauta adachokako ku Ejipito. Usiku wonse Chauta adachezera kutulutsa Aisraelewo m'dziko lija la Ejipito. Nchifukwa chake usiku umenewu ndi wopatulikira Chauta pa mibadwo yonse, kuti ukhale usiku womwe Aisraele onse ayenera kuchezera. Tsono Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti, “Malamulo ake a Paska ndi aŵa: Mlendo aliyense asadyeko. Kapolo aliyense wochita kugulidwa angadyeko, koma atayamba waumbalidwa. Mlendo kapena wantchito wanu aliyense asadyeko. Muzidyera m'nyumba imodzi, musatuluke nayo panja nyamayo, ndipo musaphwanye mafupa ake. Mtundu wonse wa Aisraele uzichita mwambo umenewu. Mlendo akakhala pakati panu, namafuna kuti achite nao mwambo wa Paska ya Chauta, muziyamba mwaumbala amuna onse am'banjamo. Pambuyo pake angathe kuloŵa ndi kumachita nao mwambowo. Iyeyo muzimuyesa ngati mbadwa yeniyeni ya Israele. Koma wosaumbalidwa asadyeko. Lamulo limeneli ndi la mbadwa yeniyeni ya Israele, ndiponso la mlendo woumbalidwa amene ali pakati panu.” Aisraele onse adamveradi zimenezi, ndipo ankachitadi zimene Chauta adalamula Mose ndi Aroni. Pa tsiku lomwelo ndi pamene Chauta adatulutsa Aisraele ku Ejipito mwa magulumagulu ao. Chauta adauzanso Mose kuti, “Ana onse achisamba uŵapereke kwa Ine. Pakati pa Aisraele mwana wamwamuna aliyense woyamba kubadwa kaya ndi wa munthu kaya ndi wa nyama, ndi wanga ameneyo.” Tsono Mose adauza anthu kuti, “Muzikumbukira tsiku limene mudatuluka ku Ejipito, ku dziko laukapolo, chifukwa Chauta adakutulutsani kumeneko ndi dzanja lake lamphamvu. Musadye chilichonse chofufumitsa. Mukuchoka ku Ejipito pa tsiku lalero, mwezi uno wa Abibu. Chauta adalonjeza makolo anu kuti adzakupatsani dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, Ahivi ndi Ayebusi. Dziko limenelo ndi lamwanaalirenji. Akadzakuloŵetsani m'dziko limenelo, muzidzachita mwambo umenewu mwezi uno. Pa masiku asanu ndi aŵiri, muzidzadya buledi wosafufumitsa, ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiŵirilo pazidzakhala chikondwerero cha Chauta. Muzidzadya buledi wosafufumitsa pa masiku asanu ndi aŵiri. Pasamadzakhala buledi wofufumitsa, kapena chofufumitsira chilichonse m'dziko lanu lonselo. Pa tsiku limenelo muzidzauza ana anu kuti, ‘Tikuchita zonsezi chifukwa cha zimene Chauta adatichitira pamene tinkachoka ku Ejipito.’ Lamulo limeneli lidzakhala ngati chizindikiro chomangidwa padzanja panu, kapena chikumbutso chomangidwa pamphumi panu. Motero malamulo a Chauta sadzachoka konse pakamwa panu, chifukwa Iye adakutulutsani ku Ejipito ndi dzanja lake lamphamvu. Musunge malangizo ameneŵa pa nthaŵi yake chaka ndi chaka. “Chauta adzakuloŵetsani m'dziko la Akanani limene adakulonjezani pamodzi ndi makolo anu. Akadzakupatsani dziko, muzidzapereka kwa Chauta chilichonse choyamba kubadwa. Zoŵeta zanu zamphongo zoyamba kubadwa nza Chauta zimenezo. Koma mwanawabulu woyamba kubadwa, muzimuwombolanso pakupereka mwanawankhosa m'malo mwake. Ngati simufuna kumuwombola, muzimthyola khosi. Muziwombola mwana wamwamuna wachisamba aliyense. M'tsogolo mwana wanu wamwamuna adzakufunsani kuti, ‘Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?’ Pamenepo inu mudzayankhe kuti, ‘Chauta adatitulutsa ku Ejipito, ku dziko laukapolo, ndi dzanja lake lamphamvu. Farao atauma mtima ndithu, natikaniza kuchoka, Chauta adapha mwana wachisamba aliyense wamwamuna m'dziko lonse la Ejipito. Adapha ana a anthu ndi a zoŵeta omwe. Nchifukwa chake nyama yamphongo iliyonse yoyamba kubadwa imaperekedwa nsembe kwa Chauta. Koma ana athu achisamba aamuna, timachita choombola. Chimenechi chidzakhala chikumbutso, monga ngati chizindikiro chomangidwa pa dzanja lanu kapena pamphumi panu, chifukwa Chauta adatitulutsa ku Ejipito ndi dzanja lake lamphamvu.’ ” Farao ataŵalola Aisraele kuti apite, Mulungu sadaŵadzeretse njira yopita kwa Afilisti, ngakhale kuti imeneyi inali njira yachidule. Mulungu adati, “Sindifuna kuti anthu ameneŵa adzasinthe maganizo ao nadzabwereranso ku Ejipito, akadzangokumana ndi nkhondo yolimbana nawo.” M'malo mwake Mulungu adaŵadzeretsa njira yozungulira, yachipululu, yopita ku Nyanja Yofiira. Monsemo nkuti Aisraele ali okonzekeratu za nkhondo. Mose adanyamula mafupa aja a Yosefe, chifukwa Yosefeyo anali atalumbiritsa Aisraele aja kuti ndithu mafupawo adzanyamule. Paja Yosefe adaanena kuti, “Ndithu, Mulungu adzakuthandizani, koma mudzayenera kunyamula mafupa angaŵa kuchoka nawo kuno.” Aisraele adachoka ku Sukoti, nakagona ku Etamu m'mbali mwa chipululu. Nthaŵi yamasana Chauta ankaŵatsogolera ndi chipilala chamtambo namaŵalangiza njira. Ndipo nthaŵi yausiku, ankaŵatsogolera ndi chipilala chamoto, kuŵaunikira njira kuti aziyenda masana ndi usiku womwe. Nthaŵi zonse chipilala chamtambo chinkatsogolera anthu masana, ndipo chipilala chamoto chinkaŵatsogolera usiku. Tsono Chauta adalamula Mose kuti, “Uza Aisraele abwerere, amange zithando patsogolo pa Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja, moyang'anana ndi Baala-Zefoni. Mumange zithando pamenepo m'mbali mwa nyanja. Apo Farao adzaganiza kuti, ‘Aisraele asokonezeka, akungoyendayenda m'dzikomo, azingidwa ndi chipululu.’ Ndidzamuumitsa mtima Farao, ndipo adzalondola Aisraelewo. Tsono ndikadzagonjetsa Farao pamodzi ndi gulu lonse lankhondo, ndidzalandira ulemu, ndipo Aejipito onse adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.” Choncho Aisraele adachita zonse monga momwe adaŵauzira. Atamva kuti anthu athaŵa, Farao, mfumu ya ku Ejipito, pamodzi ndi nduna zake zonse, adasintha maganizo pa za Aisraelewo. Adati, “Kodi ife tachitapo chiyani pamenepa? Talola Aisraele kuti athaŵe ndi kuleka kutitumikira.” Pamenepo Farao adakonzetsa galeta lake lankhondo, ndipo adauza asilikali ake kuti apite naye limodzi. Adatenga magaleta amphamvu 600 pamodzi ndi magaleta ena onse ndipo adaika atsogoleri pa magaleta onsewo. Chauta adaumitsa mtima Farao mfumu ya ku Ejipito, ndipo iye adalondola Aisraele, pamene Aisraele ankachoka monyada. Aejipitowo, ndiye kuti akavalo ndi magaleta a Farao, oyendetsa magaletawo, okwera pa akavalo ndi gulu lankhondo la Farao, adalondola Aisraele aja nakaŵapeza pamalo pomwe adaamanga zithando paja, pafupi ndi Pihahiroti, moyang'anana ndi Baala-Zefoni. Tsono Farao atayandikira, Aisraele aja adaona Aejipito akuŵalondola, ndipo adachita mantha kwambiri, nayamba kulira mofuula kwa Chauta. Adafunsa Mose kuti, “Kodi nchifukwa chakuti ku Ejipito kunalibe malo a manda, kuti inuyo mutifikitse kuchipululu kuno kuti tidzafe? Mwatichita chiyani potitulutsa ku Ejipito? Kodi ife tisanachoke ku Ejipito, sitidakuuzirenitu zimenezi? Ife tidaanena kuti, ‘Mutileke, tikhalebe akapolo a Aejipito.’ Zidakatikomera ife kukhalabe akapolo kupambana kuti tifere kuchipululu kuno.” Apo Mose adayankha anthuwo kuti, “Musaope! Limbikani, ndipo muzingopenya zimene Chauta achite lero lino pofuna kukupulumutsani. Aejipito amene mukuŵaona lerowo, simudzaŵaonanso. Chauta ndiye amene akumenyereni nkhondo. Inuyo simuchitapo kanthu konse.” Apo Chauta adafunsa Mose kuti, “Chifukwa chiyani ukulira kwa ine? Auze Aisraele kuti aziyenda. Tenga ndodo yakoyo, ndipo utambalitse dzanja pa nyanja, kuigaŵa nyanjayo kuti Aisraele aoloke pouma. Ndidzaŵaumitsa mtima Aejipitowo, kotero kuti adzalondola Aisraele ndithu. Ndipo kugonjetsa kumene ndidzagonjetsa Farao pamodzi ndi ankhondo ake, magaleta ake ndi oyendetsa ake omwe, ndidzapeza nako ulemerero. Aejipitowo adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, akadzaona m'mene ndipambanire Farao ndi magaleta ake ndi oŵayendetsa ake.” Apo mngelo wa Mulungu, yemwe ankatsogolera Aisraele aja, adakakhala cha kumbuyo kwao. Mtambo womwe unkakhala patsogolo pao uja, udakakhalanso chakumbuyo kwao. Unali pakati pa gulu lankhondo la Aejipito ndi gulu lankhondo la Aisraele. Choncho panali mtambo ndi mdima, kotero kuti magulu ankhondo aŵiriwo sadayandikane usiku wonse. Tsono Mose adatambalitsa dzanja lake pa nyanja, ndipo pompo Chauta adaumitsa nyanja ija, pogwiritsa ntchito mphepo yamkuntho yakuvuma, imene idaomba usiku wonse ndi kuumitsa nyanjayo. Madziwo adagaŵikana, ndipo adakhala ngati chipupa pa mbali zonse ziŵiri, motero Aisraele adaoloka pouma. Aejipito aja adalondola Aisraelewo mpaka kukaloŵa nawo m'nyanja muja. Akavalo onse a Farao adaloŵa m'nyanja, pamodzi ndi magaleta ake ndi oŵayendetsa ake omwe. Tsono kusanache m'maŵa ndithu, Chauta, ali m'chipilala chamtambo ndi chamoto, adayang'ana ankhondo a Aejipito ndipo adaŵachititsa mantha. Adapinda mikombero ya magaleta ao, kotero kuti magaletawo ankayenda movutika. Pamenepo Aejipito aja adati, “Tiyeni tiŵathaŵe Aisraeleŵa, chifukwa Chauta akuŵamenyera nkhondo, kulimbana nafe.” Apo Chauta adauza Mose kuti, “Tambalitsa dzanja lako kunyanjako kuti madziwo abwerere, ndi kumiza Aejipitowo pamodzi ndi magaleta ao ndi oŵayendetsa ake omwe.” Motero Mose adatambalitsa dzanja lake ku nyanja, ndipo m'mene kunkacha, nkuti madziwo akubwerera m'malo mwake. Aejipitowo adayesa kuthaŵa, koma Chauta adaŵabweza momwe m'nyanjamo. Ndipo madziwo adabwerera, namiza magaleta aja ndi oŵayendetsawo, pamodzi ndi gulu lonse lankhondo la Farao lija linkaŵatsatali. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adapulumuka. Koma Aisraele onse aja adaoloka nyanjayo pansi pali pouma, madzi atangoima pa mbali zonse ziŵiri. Pa tsiku limenelo, Chauta adapulumutsa Aisraele kwa Aejipito. Aisraele adaona Aejipitowo ali ngundangunda m'mbali mwa nyanja. Choncho adaona mphamvu zazikulu zimene Chauta adaonetsa pogonjetsa Aejipito aja. Tsono adayamba kuwopa Chauta, ndipo ankakhulupirira Chautayo ndi Mose mtumiki wake. Tsono Mose pamodzi ndi Aisraele aja adaimba nyimbo iyi, kuimbira Chauta, adati, “Ndidzaimbira Chauta chifukwa choti wapambana, waponya m'nyanja akavalo pamodzi ndi okwerapo omwe. Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye chipulumutso changa. Iye ndiye Mulungu wanga, ndipo ndidzamtamanda. Ndiye Mulungu wa atate anga, ndipo ndidzamuyamika kwakukulu. Chauta ndi wankhondo, Chauta ndilo dzina lake. “Chauta adaponya m'nyanja magaleta a Farao pamodzi ndi gulu lake lankhondo, adammizira atsogoleri ake amphamvu m'Nyanja Yofiira. Nyanja yozamayo idaŵaphimba onse, adamira mpaka pansi pa nyanja ngati miyala. Inu Chauta dzanja lanu lamanja ndi laulemerero, chifukwa cha nyonga zake, dzanja lanu lamanja limatswanya adani. Mumagonjetsa adani anu ndi ulemerero wanu wopambana. Ukali wanu woyaka ngati moto ukuŵatentha ngati mapesi. Mutauzira mpweya wanu, madzi adaunjikana pa malo amodzi. Madzi oyenda adangoima kuti chilili, ngati khoma. Nyanja yozamayo idalimba mpaka pansi pake. Mdani uja adati, ‘Ndidzaŵalondola nkuŵagwira. Chuma chao ndidzachigaŵagaŵa, ndipo mtima wanga udzakhutira nacho. Ndidzasolola lupanga, ndipo ndidzaŵaononga ndi dzanja langa.’ Koma Inu mudangouzira ndi mphepo yanu, ndipo nyanja idaŵamiza. Adangomira ngati chitsulo mpaka pansi pa madzi. “Inu Chauta, kodi pali mulungu wina wofanafana nanu? Ndani amafanafana ndi Inu, amene muli aulemu chifukwa cha ungwiro wanu? Ndani amafanafana nanu, Inu amene muli oopsa chifukwa cha ntchito zanu zaulemu ndi zodabwitsa? Mudatambalitsa dzanja lanu lamanja, ndipo nthaka idaŵameza. “Koma anthu amene mudaŵaombola, mudaŵatsogolera ndi chikondi chanu chosasinthika. Mudaŵatsogolera ku malo anu oyera ndi mphamvu zanu. Anthu a mitundu ina amva mbiriyi, ndipo anjenjemera ndi mantha. Mantha oopsa aŵagwira Afilisti. Tsopano lino mafumu a ku Edomu ataya mtima. Atsogoleri a ku Mowabu ayambapo kunjenjemera. Onse a ku Kanani agooka m'nkhongono. Onsewo agwidwa ndi mantha oopsa. Iwo akhala chete ngati mwala, chifukwa cha kuwopa mphamvu zanu zazikulu. Angokhala chete mpaka anthu anu, Inu Chauta, atabzola, anthu amene mudaŵaombola mu ukapolo. Mudzaŵaloŵetsa ndi kuŵakhazika pa phiri lanu, pa malo amene Inu Chauta mudaŵapanga kuti akhale anu, m'nyumba yopembedzera imene Inu mudaimanga. Chauta adzakhala mfumu mpaka muyaya.” Pamene akavalo a Farao, pamodzi ndi magaleta ndi okwerapo ake omwe, adaloŵa m'nyanja, Chauta adaŵabweza madziwo, ndipo adamiza onsewo. Koma Aisraele adayenda pouma m'kati mwa nyanjayo. Miriyamu, mneneri wamkazi, mlongo wa Aroni, adatenga kang'oma, ndipo akazi onse adamtsata pambuyo akuimba ting'oma, ndi kumavina. Ndipo Miriyamu adaŵaimbira iwowo nyimbo yakuti, “Imbirani Chauta chifukwa wapambana, waponya m'nyanja akavalo pamodzi ndi okwerapo ake omwe.” Tsono Mose adatsogolera Aisraele ku Nyanja Yofiira kuja nakaloŵa m'chipululu cha Suri. Adayenda m'menemo masiku atatu, osapeza madzi. Ndipo adakafika ku Mara, koma kumeneko madzi ake anali oŵaŵa, kotero kuti sadathe kuŵamwa. Nchifukwa chake malowo adaŵatcha kuti Mara. Apo anthu aja adadandaulira Mose, namufunsa kuti, “Kodi ife timwa chiyani?” Tsono Mose adapemphera dzolimba kwa Chauta, ndipo Chauta adamuwonetsa kamtengo. Mose adaponya kamtengoko m'madzi, ndipo madziwo adaleka kuŵaŵako. Kumeneko Chauta adapatsa anthuwo lamulo lokhazikika, ndipo adaŵayesanso komweko. Adati, “Mukamandimvera Ine Chauta, Mulungu wanu, kumachita zolungama, kumasamala malamulo anga ndi kumamvera zimene ndikukulamulani, sindidzakulangani ndi nthenda zilizonse zimene ndidalanga nazo Aejipito. Ine ndine Chauta amene ndimakuchiritsani.” Pambuyo pake adakafika ku Elimu kumene kunali akasupe khumi ndi aŵiri, ndi mitengo ya migwalangwa makumi asanu ndi aŵiri. Tsono adamanga mahema ao kumeneko pafupi ndi madzi. Pambuyo pake khamu lonse la Aisraele lidayamba ulendo kuchokera ku Elimu, ndipo pa tsiku la 15 la mwezi wachiŵiri atachoka ku Ejipito, adafika ku chipululu cha Sini, chimene chili pakati pa Elimu ndi Sinai. Ndipo khamu lonse lidadandaulira Mose ndi Aroni m'chipululu muja kuti, “Kukadakhala bwino Chauta akadatiphera ku Ejipito konkuja, kumene tinkakhala tikudya nyama ndi buledi, ndipo tinkakhuta. Koma inu mwatifikitsa kuchipululu kuno kuti mutiphe tonse ndi njala.” Apo Chauta adauza Mose kuti, “Chabwino, ndikupatsani chakudya chimene chidzagwa ngati mvula kuchokera kumwamba. Anthu azituluka tsiku ndi tsiku kukatola chakudya chokwanira tsiku limodzi, kuti ndiŵayese ndipo ndiwone ngati adzayenda motsata malamulo anga kapena ai. Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi, pokonza chimene adatola adzapeza kuti nchokwanira masiku aŵiri.” Tsono Mose ndi Aroni adauza Aisraele onse kuti, “Madzulo omwe ano mudzadziŵa kuti ndi Chauta amene adakutulutsani ku Ejipito, m'maŵa mwake mudzaona ulemerero wa Chauta. Wamva madandaulo anu omuŵiringulira aja. Kodi ife ndife yani, kuti inu muzitiŵiringulira?” Ndipo Mose adati, “Ndi Chauta amene adzakupatsani madzulo nyama yoti mudye, ndi m'maŵa buledi woti nkukhuta, chifukwa choti wamva madandaulo anu onse omuŵiringulira aja. Ife ndife yani? Madandaulo anu simudaŵiringulire ife ai, koma Chauta.” Pamenepo Mose adauza Aroni kuti akauze anthuwo kuti, “Bwerani, mudzaime pamaso pa Chauta chifukwa wamva madandaulo anu onse.” Tsono Aroni akulankhula ndi khamu lonse lija, khamulo lidatembenuka kupenya ku chipululu, ndipo ulemerero wa Chauta udaoneka mu mtambo mwadzidzidzi. Chauta adauza Mose kuti, “Ndamva madandaulo a Aisraele. Ndiye uŵauze kuti, ‘Madzulo mudzadya nyama, ndipo m'maŵa mudzadya buledi, choncho mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.’ ” Motero madzulo kudagwa zinziri, ndipo zidadzaza ponseponse pamahemapo. M'maŵa ndithu padagwa mame ponse pozungulira mahemawo. Mamewo atangokamuka, panthakapo m'chipululu muja padapezeka tinthu tina topyapyala, tambee ngati chipale, ndiponso tonyata. Aisraele ataona tinthuto sadatidziŵe kuti nchiyani, mwakuti adayamba kufunsana kuti “Kodi timeneti ntiyani?” Mose adaŵauza kuti, “Ameneyu ndi buledi yemwe Chauta wakupatsani kuti mudye. Chauta walamula kuti aliyense mwa inu atole womukwanira kudya, ndiye kuti malita aŵiri pa munthu mmodzi, malinga ndi chiŵerengero cha anthu onse a m'hema mwake.” Aisraele adachitadi zimenezo. Ena adatola tambiri, koma ena pang'ono. Tsono atayesa ndi muyeso wa malita aŵiri, adaona kuti amene adaatola tambiri, sitidaŵatsalireko, amene adaatola pang'ono, sitidaŵathere. Aliyense adangotola tokwanira. Pamenepo Mose adaŵauza kuti, “Munthu aliyense asasungeko mpaka m'maŵa.” Komabe ena mwa iwowo sadamvere zimene adaanena Mosezo, adasungako mpaka m'maŵa mwake. Koma kutacha, adaona kuti tonseto tagwa mphutsi, ndipo tikununkha. Apo Mose adaŵapsera mtima anthuwo. Ankatola m'maŵa mulimonse, ndipo aliyense ankatola monga m'mene ankasoŵera. Koma dzuŵa likatentha, tinthuto tinkasungunuka. Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi ankatola chakudya cha masiku aŵiri, chokwanira malita anai ndi theka pa munthu mmodzi. Ndipo atsogoleri onse a Aisraele adabwera kwa Mose kudzamuuza zimenezo. Tsono Mose adaŵauza kuti, “Chauta walamula kuti, ‘Maŵa ndi tsiku lopumula, tsiku la Sabata, loperekedwa kwa Chauta. Wotchani yense amene mufuna kuwotcha, ndipo muphike yense amene mufuna kuphika. Wotsalako mumsunge padera mpaka maŵa.’ ” Mose atalamula zimenezi, anthuwo adasungadi totsalato mpaka m'maŵa mwake tosaonongeka, ndipo sitidagwe mphutsi. Pambuyo pake Mose adauza anthuwo kuti, “Idyani ameneyu lero, chifukwa lero ndi tsiku la Sabata loperekedwa kwa Chauta. Lero simumpezatu kunjaku. Mutole chakudya pa masiku asanu ndi limodzi. Koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, tsiku la Sabata, chakudyacho sichidzapezeka.” Pa tsiku lachisanu ndi chiŵirilo anthu ena adaapita kuti akatole chakudya, koma sadachipeze. Pamenepo Chauta adafunsa Mose kuti, “Kodi mudzakhalabe osamvera mau anga ndi malamulo anga mpaka liti? Kumbukirani kuti ndine Chauta, amene ndidakupatsani tsiku la Sabata. Tsono chifukwa cha chimenechi ndimakupatsani chakudya chokwanira masiku aŵiri pa tsiku lachisanu ndi chimodzi. Aliyense azingokhala komwe aliriko pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri. Asachoke ndi mmodzi yemwe pakhomo pake.” Motero anthu sankagwira ntchito pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri. Aisraele chakudyacho adachitcha mana. Maonekedwe ake anali onga njere zamapira, ndiponso oyera. Pakudya, ankazuna ngati buledi wopangidwa ndi uchi. Tsono Mose adati, “Chauta walamula kuti ‘Musungeko mana ena kuti zidzukulu zanu zidzaone chakudya chimene ndidakupatsani m'chipululu, nditakutulutsani ku Ejipito kuja.’ ” Ndipo Mose adauza Aroni kuti, “Tenga mtsuko, uikemo mana wokwana malita aŵiri. Utatero uike pamaso pa Chauta kuti manayo asungike chifukwa cha zidzukulu zanu.” Monga momwe Chauta adalamulira Mose, Aroni adaika mtsukowo patsogolo pa bokosi lachipangano, kuti manayo asungike. Aisraelewo adakhala alikudya mana zaka makumi anai, mpaka adakafika kudziko kokhala anthu. Adadya mana mpaka adafika ku malire a dziko la Kanani. Malita aŵiri alingana ndi gawo lachikhumi la efa. Khamu lonse la Aisraele lija lidachoka ku chipululu cha Sini kuja, ndipo linkangoyenda kuchoka pa chigono china mpaka pa chigono chinanso, monga momwe Chauta ankalamulira. Tsono adakamanga mahema ku Refidimu. Kumeneko kunalibe madzi akumwa. Ndiye anthuwo adayamba kukangana ndi Mose, namanena kuti, “Tipatseni madzi akumwa.” Mose adaŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukukangana ndi ine? Chifukwa chiyani mukuyesa Chauta?” Koma anthu aja anali ndi ludzu loopsa, ndipo ankangoŵiringulira Mose, kuti “Chifukwa chiyani mudatitulutsa ku Ejipito kuti mutiphe ndi ludzu, ife pamodzi ndi ana athu ndi zoŵeta zathu?” Apo Mose adapemphera mokweza mau kwa Chauta, adati, “Kodi anthu ameneŵa ndichite nawo chiyani? Iwowo ngokonzeka kundiponya miyala.” Pamenepo Chauta adauza Mose kuti, “Tengako atsogoleri ena a Aisraele, mukakhale patsogolo pa anthuwo. Tsono utenge ndodo udamenya nayo madzi a mu mtsinje wa Nailo ija, ndipo upite. Ine ndidzakhala patsogolo pako kumeneko pafupi ndi thanthwelo, pa phiri la Horebu. Ukamenye thanthwe, tsono mudzatuluka madzi m'thanthwemo, kuti anthuwo amwe.” Mose adachitadi zimenezo pamaso pa atsogoleri a Aisraele aja. Malowo adaŵatcha Mayeso ndiponso Makangano, chifukwa Aisraele adakangana ndi Mose, ndipo adayesa Chauta pofunsa kuti, “Kodi Chauta ali nafe, kapena ai?” Tsono kudabwera Aamaleke ku Refidimu kudzamenyana ndi Aisraele. Mose adauza Yoswa kuti, “Tisankhulireko amuna ena, maŵa mupite kukamenyana nawo nkhondo Aamaleke. Ine ndidzaimirira pamwamba pa phiri, nditagwira ndodo adandipatsa Mulungu ija.” Yoswa adachitadi monga momwe Mose adalamulira, adatuluka kukamenyana ndi Aamalekewo. Nthaŵi yomweyo Mose, Aroni ndi Huri adakwera pamwamba pa phiri. Mose ankati akakweza manja ake, Aisraele ankapambana pa nkhondoyo, koma akatsitsa pansi manja, Aamaleke ankapambana. Tsono manja a Mose atatopa, Aroni pamodzi ndi Huri uja adatenga mwala namkhazikira Mose kuti akhalepo. Aŵiriwo adakhala wina uku wina uku, atagwirira manja a Mose aja. Adaŵagwirira ndithu mpaka dzuŵa kuloŵa. Ndipo Yoswa adagonjetseratu kwathunthu Aamalekewo. Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Zimenezi muzilembe m'buku kuti zidzakumbukike, ndipo munene pamaso pa Yoswa kuti Aamalekewo adzafafanizika kwathunthu.” Ndipo Mose adamanga guwa nalitcha kuti, “Chauta ndiye mbendera yanga.” Adati, “Kwezetsani mbendera ya Chauta! Chauta adzapitirirabe kumenya nkhondo ndi Aamaleke mpaka muyaya.” Yetero, wansembe wa ku Midiyani, mpongozi wake wa Mose, adamva zonse zija zimene Mulungu adachitira Mose ndiponso anthu ake Aisraele. Adamvanso za m'mene Chauta adaŵatulutsira ku Ejipito. Motero adabwera ndi Zipora, mkazi wa Mose, amene Moseyo anali atamsiya. Yetero adabweranso ndi ana aamuna aŵiri aja a Zipora. Mwana woyamba Mose adaamutcha Geresomo (chifukwa adati, “Ndakhala mlendo m'dziko lachilendo.”) Mwana wake wachiŵiri Mose adaamutcha Eliyezere, (chifukwa adati, “Mulungu wa atate anga ndiye thandizo langa, ndipo adandipulumutsa ku lupanga la Farao.”) Yeteroyo adabwera ndi mkazi wa Mose ndi ana ake aamuna kuchipululu kuja, ku malo amene Mose adamangako mahema, pa phiri la Mulungu. Munthu wina adakauza Mose kuti, “Mpongozi wanu Yetero akubwera ndi mkazi wanu ndi ana anu aŵiri aamuna.” Tsono Mose adamchingamira nakakumana naye, ndipo adamgwadira ndi kumumpsompsona. Atalonjerana ndi kufunsana za moyo, adakaloŵa mu hema. Ndipo Mose adamufotokozera zonse zimene Chauta adamchita Farao ndi Aejipito chifukwa cha Aisraelewo. Adamsimbiranso za mavuto omwe adaakumana nawo pa njira, ndi zonse zimene Chauta adaachita poŵapulumutsa. Yetero adakondwa kwambiri ndi ntchito zabwino zimene Chauta adaachitira Aisraele pakuŵapulumutsa kwa Aejipito. Tsono adati, “Mtamandeni Chauta amene adakupulumutsani kwa Aejipito ndi kwa Farao. Mtamandeni Chauta amene adapulumutsa anthu ake ku ukapolo wa Aejipito. Tsopano ndikudziŵa kuti Chauta ndi wamkulu kupambana milungu ina yonse, chifukwa adapulumutsa Aisraele kwa Aejipito, pamene Aejipitowo ankaŵanyoza.” Pamenepo Yetero adapereka kwa Mulungu nsembe yopsereza ndi nsembe zinanso. Kenaka Aroni ndi atsogoleri a Aisraele adabwera pamaso pa Mulungu kudzadya pamodzi ndi Yetero mpongozi wa Mose. M'maŵa mwake Mose adayamba kuweruza milandu ya anthu. Ndipo anthuwo ankabwera ndi milandu yao kwa Moseyo kuyambira m'maŵa mpaka usiku. Yetero mpongozi wake wa Mose ataona zonse zimene Moseyo ankachita, adafunsa kuti, “Kodi zonse zimene mukuchitira anthuzi nzotani? Chifukwa chiyani mukukhala nokha pano, pamene anthu akubwerabe kwa inu kuyambira m'maŵa mpaka usiku?” Mose adayankha kuti, “Ndiyenera kuchita zimenezi chifukwa choti anthu amabwera kwa ine, kuti amve zimene Mulungu afuna. Anthu aŵiri akamakangana, amabwera kwa ine, ndipo ndimaŵaweruza, ndi kuwona kuti wakhoza ndani. Ndipo ndimaŵauza mau a Mulungu ndi malamulo ake.” Apo Yetero mpongozi wa Moseyo adati, “Simukuchita bwino ai. Inu mudzafooka msanga, pamodzi ndi anthu muli nawoŵa. Ntchito imeneyi njaikulu kuposa mphamvu zanu, ndipo simungaithe nokha. Tandimverani tsono, ndikulangizeni, ndipo Mulungu adzakhala nanu. Inu muyenera kuima m'malo mwa anthu pamaso pa Mulungu ndi kubwera ndi makangano ao kwa Iye. Muyenera kuŵaphunzitsa mau ndi malamulo a Mulungu, ndi kuŵafotokozera m'mene azikhalira ndi m'mene azichitira. Komanso sankhulani amuna anzeru, ndipo muŵaike kuti akhale atsogoleri a anthu, motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 100, ena a anthu 50, ena a anthu khumi chabe. Ayenera kukhala anthu oopa Mulungu, okhulupirika, ndiponso osakopeka ndi ziphuphu. Iwo ndiwo aziweruza anthu nthaŵi zonse. Azibwera ndi milandu yovuta yokha kwa inu, koma timilandu ting'onoting'ono aziweruza okha. Adzakuchepetserani ntchito iwowo pakusenza katunduyo pamodzi nanu. Mukachita zimenezi monga Mulungu akulamulira, simudzafooka, ndipo anthu onseŵa adzatha kumabwerera kwao, zao zonse zitakonzeka.” Mose adamvera zonse zimene adanena Yetero zija. Adasankha anthu anzeru pakati pa Aisraelewo ndi kuŵaika kuti akhale atsogoleri a anthu motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 100, ena a anthu 50, ena a anthu khumi chabe, ndipo iwowo ankaweruza anthu nthaŵi zonse. Milandu yovuta yokha ankabwera nayo kwa Mose, koma timilandu ting'onoting'ono ankangomaliza okha. Tsono Yeteroyo atalaŵirana naye Mose, adabwerera kwao. Pa tsiku loyamba la mwezi wachitatu chichokere cha Aisraele ku Ejipito, mpamene adafika ku chipululu cha Sinai. Atachoka ku Refidimu adakafika ku chipululu cha Sinai, kumene adamangako mahema pafupi ndi phirilo. Mose adakwera phiri kukakumana ndi Mulungu, ndipo Mulungu adamuitana m'phirimo namuuza kuti, “Uuze zidzukulu za Yakobe, ndiye kuti mtundu wonse wa Aisraele kuti, ‘Mudaona zimene ndidaŵachita Aejipito, ndiponso muja ndidakunyamulani monga m'mene mphungu imanyamulira ana ake pa mapiko ake, ndipo ndidakufikitsani kwa Ine. Tsono mukamandimvera ndi kusunga chipangano changa, mudzakhala anthu anga pakati pa makamu onse, pakuti dziko lonse lapansi ndi langa. Ndipo inu mudzakhala anthu onditumikira Ine ngati ansembe, ndiponso ngati mtundu woyera. Tsono ukaŵauze mau ameneŵa Aisraele.’ ” Pamenepo Mose adakaitana atsogoleri a Aisraele, ndipo adaŵauza zonse zimene Chauta adamlamula. Anthuwo adayankha pamodzi kuti, “Tidzachita zonse zimene Chauta wanena.” Pambuyo pake Mose adakafotokozera Chauta zimene anthuwo adanena. Chauta adauza Mose kuti, “Ndikubwera kwa iwe mu mtambo wochindikira, kuti anthuwo azidzandimva ndikamalankhula ndi iwe, ndiponso kuti adzakhulupirire nthaŵi zonse.” Tsono Mose adauza Chauta zimene anthu adanena. Chauta adauza Mose kuti, “Pita kwa anthuwo, ndipo uŵayeretse lero ndi maŵa. Achape zovala zao, ndipo akhale okonzeka mkucha. Pa tsiku limenelo, Ine Chauta ndidzatsika pa phiri la Sinai, ndipo kumeneko anthu onse adzandiwona Ine. Uŵalembere malire anthuwo pozungulira phirilo, ndipo uŵauze kuti, ‘Samalani, musakwere phiri kapena kukhudza tsinde lake. Wina aliyense akalikhudza, afa. Wina aliyense asakhudze munthuyo, koma anthu amponye miyala kapena kumubaya. Chikhale choŵeta, chidzaphedwa; akhale munthu, adzaphedwanso. Mbetete ikamalira, anthu abwere ku phiri.’ ” Mose adatsika phiri, nakafika kwa anthuwo, ndipo adaŵayeretsa. Anthuwo adachapadi zovala zao. Kenaka Mose adaŵauza kuti, “Mkucha uno, mukonzeke. Musayandikize mkazi.” Tsono m'maŵa, pa tsiku lakelo, panali mabingu ndi mphezi paphiripo. Kunalinso mtambo wochindikira, ndiponso kulira kwakukulu kwa mbetete. Anthu onse m'mahemamo ankangonjenjemera ndi mantha. Mose adaŵatsogolera anthuwo kuchoka kumahemako, kuti akakumane ndi Mulungu, ndipo onsewo adaima patsinde pa phiri. Phiri lonse la Sinai lidaphimbidwa ndi utsi, chifukwa choti Mulungu adaatsikira paphiripo. Utsiwo unkangokwera ngati utsi wam'ng'anjo, ndipo anthu onse aja ankangonjenjemera kwambiri. Liwu la mbetete linkakulirakulira. Apo Mose adalankhula, ndipo Mulungu adamuyankha ndi mabingu. Chauta adafika pamwamba pa phiri la Sinai, adaitana Mose pamwamba pa phiri, ndipo Moseyo adakwera phirilo. Chauta adauza Mose kuti, “Tsika pansi, ndipo uza anthu kuti asapitirire malire ndi kubwera kumadzayang'ana kwa Ine, kuti ambiri mwa iwowo angadzafe. Ngakhale ansembe amene akufika pafupi ndi Ine adziyeretse, kuti ndingadzaŵalange.” Mose adayankha Chauta kuti, “Anthuwo sangakwere ai, chifukwa mudachenjezeratu kuti, ‘Mulembe malire kuzungulira phirilo, ndipo mulipatule kuti likhale loyera.’ ” Tsono Chauta adauza Moseyo kuti, “Tsika pansi, ndipo ukamtenge Aroni, ubwere naye kuno. Koma ansembe pamodzi ndi anthu asabzole malirewo kubwera kwa Ine kuno, kuti ndingadzaŵalange.” Apo Mose adatsikira kwa anthu kuja kukaŵauza zimenezo. Tsono Mulungu adalankhula mau onseŵa, adati, “Ine ndine Chauta Mulungu wako, amene ndidakutulutsa mu ukapolo ku dziko la Ejipito. “Usakhale ndi milungu ina, koma Ine ndekha. “Usadzipangire fano kapena chithunzi chilichonse chofanizira kanthu kena kalikonse kakumwamba kapena ka pa dziko lapansi, kapenanso ka m'madzi a pansi pa dziko. Usagwadire fano lililonse kapena kumalipembedza, chifukwa Ine Chauta, Mulungu wako, ndine Mulungu wosalola kupikisana nane, ndipo ndimalanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai. Komatu anthu ambirimbiri a mibadwo yosaŵerengeka amene amandikonda, namatsata malamulo anga, ndimaŵakonda ndi chikondi chosasinthika. “Usatchule pachabe dzina la Chauta, Mulungu wako, chifukwa Mulunguyo sadzamleka aliyense wotchula pachabe dzina lakelo. “Uzikumbukira tsiku la Sabata, uzilisunga loyera. Masiku asanu ndi limodzi uzigwira ntchito zako zonse. Koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi la Sabata loperekedwa kwa Chauta, Mulungu wako. Usamagwira ntchito pa tsiku limenelo iweyo, kapena ana ako, kapena antchito ako, kapena zoŵeta zako, kapena mlendo amene amakhala m'mudzi mwako. Paja pa masiku asanu ndi limodzi Chauta adalenga zonse zakumwamba, za pa dziko lapansi, nyanja ndi zinthu zonse zam'menemo, koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri adapumula. Nchifukwa chake Chauta adadalitsa tsiku la Sabata, nalisandutsa loyera. “Uzilemekeza atate ndi amai ako, kuti masiku a moyo wako achuluke m'dziko limene Chauta, Mulungu wako, akukupatsa. “Usaphe.” “Usachite chigololo.” “Usabe.” “Usachite umboni womnamizira mnzako.” “Usasirire nyumba ya mnzako. Usasirire mkazi wa mnzako, kapena wantchito wake wamwamuna kapena wantchito wake wamkazi, kapena ng'ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.” Anthu onse ankamva mabingu ndi kulira kwa lipenga, namaona mphezi ndi utsi paphiripo, ndipo ankaopa ndi kunjenjemera, ataima kutali. Adauza Mose kuti, “Muzilankhula ndi ife ndinu, ndipo tidzamva. Mulungu asalankhule nafe, kuti tingafe.” Apo Mose adaŵayankha kuti, “Musaope, Mulungu wafika kuti akuyeseni, kuti muzimuwopa m'mitima mwanu, ndiponso kuti musachimwe.” Koma anthu ankaima kutali, Mose yekha ndiye adayandikira mtambo wamdima m'mene munali Mulungu. Ndipo Chauta adalamula Mose kuti, “Kauze Aisraele kuti, ‘Mwapenyatu kuti Ine Mulungu ndalankhula nanu ndili kumwamba. Musadzipangire milungu yasiliva kapena yagolide, kuti muziipembedzera kumodzi ndi Ine. Mundimangire guwa ladothi, ndipo pamenepo muziperekapo nsembe zanu zopsereza, ndi zopereka zanu zamtendere, nkhosa ndi ng'ombe zanu. Pa malo onse amene ndikuuzani kuti muzindipembedzerapo, Ine ndidzabwera kudzakudalitsani. Mukadzandimangira guwa lamiyala, miyala yake musadzaseme, chifukwa mukadzaisema ndi chitsulo chosemera, mudzaipitsa guwalo. Popita ku guwa langa, musadzaponde pa makwerero, kuti maliseche anu angaonekere.’ ” “Tsono Aisraele uŵalangize izi: Mukagula kapolo wachihebri, adzakugwirirani ntchito zaka zisanu ndi chimodzi zokha. Muzidzammasula pa chaka chachisanu ndi chiŵiri, iye osalipirapo kanthu. Akakhala kuti anali yekha, adzachokanso yekha. Koma ngati anali ndi mkazi pobwerapo, mkazi wakeyo adzapita naye limodzi. Ngati mbuyake adampatsa mkazi, ndipo adamubalirapo ana aamuna kapena aakazi, mkaziyo pamodzi ndi anawo onse ndi a mbuyakeyo. Tsono mwamuna yekhayo ndiye adzachoke. Koma kapoloyo akanena kuti, ‘Ndimakonda mbuyanga, mkazi wanga ndi ana anga, sindifuna kuti ndimasulidwe,’ pamenepo mbuyakeyo abwere ndi kapoloyo ku Nyumba ya Mulungu. Abwere naye ku chitseko kapena ku mphuthu ya chitseko, ndipo amuboole khutu lake. Motero adzakhala kapolo wa mbuyakeyo moyo wake wonse. “Munthu akagulitsa mwana wake wamkazi ku ukapolo, mwanayo sadzaomboledwa monga m'mene amachitira ndi akapolo aamuna. Ngati mkaziyo amuipira m'maso mbuye amene ankafuna kumkwatirayo, amlole kuti aomboledwe. Sangathe konse kumgulitsa kwa anthu achilendo chifukwa chakuti sadamchite zokhulupirika. Akaganiza zopatsa mwana wake mkaziyo, azidzamsunga ngati mwana wake wamkazi ndithu. Akakwatira mkazi wina, ayenera kupitirira kumpatsa woyambayo chakudya ndi zovala. Azimlolanso zonse zomuyenera ngati mkazi wake, monga ankachitira kale. Akapanda kumchitira zimenezi, ammasule kuti akhale mfulu, koma osalandirapo ndalama. “Munthu aliyense amene amenya mnzake namupha, nayenso aphedwe ndithu. Koma ikakhala ngozi, kuti sadaganize konse zomupha mnzakeyo, angathe kuthaŵira ku malo amene ndidzakupatsani. Koma munthu akapha mnzake mwadala mwa njira yonyenga, aphedwe ndithu ngakhale wathaŵira ku guwa langa. “Munthu aliyense amene amenya bambo wake kapena mai wake, aphedwe. “Munthu aliyense amene aba munthu mnzake ndi kumgulitsa kapena kungomsunga ngati kapolo, aphedwe. “Munthu aliyense wotemberera bambo wake kapena mai wake, aphedwe. “Anthu akamenyana, ndipo wina mwa iwowo amenya mnzake ndi mwala kapena nkhonya, koma osamupha mnzakeyo, munthu womenyedwayo akadwala nakagona pa bedi, koma pambuyo pake adzuka nkumayendayenda kunja, ngakhale kuti akuyenda ndi ndodo, munthu amene adammenyayo sadzalangidwa molipsira, koma adzangolipira chifukwa cha nthaŵi yotayika pa bedi ija. Ndipo adzayenera kumsamala ndithu mnzakeyo mpaka atachira. “Munthu akamenya kapolo wake wamwamuna kapena wamkazi ndi ndodo, ndipo kapoloyo afera pomwepo, munthuyo adzalangidwa. Koma kapoloyo akakhala moyo tsiku lathunthu kapena masiku aŵiri, mbuyakeyo asalangidwe. Kapoloyo ndi chuma cha mbuyakeyo. “Anthu aamuna akamayambana, ndipo nkupweteka mai wapathupi, maiyo napititsa padera, koma osafa, amene adampwetekayo adzalipira mtengo uliwonse umene mwamuna wa maiyo angadzatchule. Ndipo adzalipira monga momwe anthu oweruza anganenere. Koma maiyo akampweteka, chilango chake chidzakhala chotere: moyo kulipa moyo, diso kulipa diso, dzino kulipa dzino, dzanja kulipa dzanja, phazi kulipa phazi, kutentha ndi moto kulipa kutentha ndi moto, bala kulipa bala, ndipo mkwingwirima kulipa mkwingwirima. “Munthu akamenya kapolo wamwamuna kapena wamkazi pa diso, nkulikoloola disolo, ammasule kapoloyo, kuti akhale mfulu chifukwa cha disolo. Akamchotsa dzino, ammasule kapoloyo, kuti akhale mfulu chifukwa cha dzinolo. “Ng'ombe ikapha munthu wamwamuna kapena wamkazi ndi nyanga, iponyedwe miyala, ndipo nyama yake musadye. Koma mwiniwake wa ng'ombeyo asalangidwe. Koma ngati khalidwe lake la ng'ombeyo linali kumangogunda anthu, ndipo mwiniwake adachenjezedwa, koma iye osaimanga, ng'ombeyo ikapha munthu wamwamuna kapena wamkazi, iponyedwe miyala ndithu. Ndipo mwiniwakeyonso aphedwe. Koma ngati amlamula kuti adziwombole, adzayenera kulipira ndalama, kuti apulumutse moyo wake. Ng'ombe ikapha mnyamata kapena mtsikana, lamulo lake ndi lomwelo ndithu. Ng'ombe ikapha kapolo wamwamuna kapena wamkazi, mwini ng'ombeyo alipe mwiniwake wa kapoloyo masekeli asiliva makumi atatu, ndipo ng'ombe iphedwe ndi miyala. “Munthu akasiya dzenje lapululu, kapena akakumba dzenje, koma osaphimbira, tsono ng'ombe kapena bulu nkugweramo, ayenera kulipira chifukwa cha choŵetacho. Alipire ndalama kwa mwini choŵetacho, koma nyamayo atenge ikhale yake. “Ng'ombe ya munthu wina ikapha ng'ombe ya mnzake, anthu aŵiriwo agulitse ng'ombe yamoyoyo, ndipo ndalama zake agaŵane. Nyama yake ya ng'ombe yakufayo agaŵanenso. Koma kukadziŵika kuti ng'ombeyo inkangogunda anthu, mwiniwake osaimanga, mwiniwakeyo ayenera kulipira pakupereka ng'ombe yamoyo chifukwa cha yakufayo. Tsono ng'ombe yakufayo ikhale yake. “Munthu akaba ng'ombe kapena nkhosa, nkuipha kapena kuigulitsa, alipire ng'ombe zisanu pa ng'ombe imodzi, kapena nkhosa zinai pa nkhosa imodzi. “Ngati mbala ipezeka ikuthyola nyumba ndipo ikanthidwa nkufa, asalipsire magazi chifukwa cha mbalayo. Koma ikaphedwa dzuŵa litatuluka, apo padzakhala kulipsira magazi. Pajatu wakuba aliyense ayenera kulipira ndithu. Ngati mbala igwidwa, ndipo ilephera kulipira mlandu, aigulitse chifukwa cha kubako. Ngati chinthu yabacho chipezeka chamoyo m'manja mwake, kaya ndi ng'ombe, kaya ndi bulu, kaya ndi nkhosa, mbalayo ilipire moŵirikiza. “Munthu akamalekerera zoŵeta zake kuloŵa m'munda mwa munthu wina ndi kukadya mbeu za m'mundamo, mwini zoŵetayo alipire mbeu zabwino kwambiri za m'munda mwake, kapena mphesa zake zabwino kwambiri. “Moto ukabuka mpaka kukafika ku thengo, ndipo ukatentha mulu wa tirigu kapena tirigu wosadula kapena munda umene uli ndi mbeu, amene adatenthayo alipire zoonongekazo. “Munthu akasungiza mnzake ndalama kapena zina zamtengowapatali, ndipo zibedwa m'nyumba mwa munthumo, mbalayo ilipire moŵirikiza. Mbalayo ikapanda kupezeka, mwini nyumba uja atengedwe ndi kufika naye pamaso pa Mulungu, kuti ziwoneke ngati katunduyo sadatenge ndi iyeyo. “Pakakhala mkangano wina uliwonse pa za chinthu cha mwiniwake kaya ndi ng'ombe, bulu, nkhosa, zovala kapena china chilichonse chotayika, chimene wina akuti nchake, anthu aŵiriwo abwere nawo pamaso pa Mulungu. Amene Mulungu ampeze kuti ndiye wolakwa, adzalipira mnzakeyo moŵirikiza. “Munthu akapereka ng'ombe, nkhosa kapena choŵeta chilichonse kwa munthu wina kuti amsungire, tsono choŵeta chija nkufa, kapena kupweteka kapena kutengedwa, wina osaona, zitsimikizike pakulumbiritsa wosungayo pamaso pa Chauta kuti sadatenge chamwinicho. Ngati sichidabedwe, mwini wakeyo adzangoti zagwa zatha, ndipo wosungayo asalipire. Koma ngati choŵetacho chidabedwa, mwiniwakeyo adzalipidwa. Ngati chidajiwa ndi zilombo, atengeko zotsalira zake kuti zikhale mboni, koma asalipire chimene chidajiwa ndi zilombocho. “Munthu akabwereka choŵeta kwa mnzake, tsono choŵeta chija nkupweteka mpaka kufa pamene sichili kwa mwiniwakeyo, wobwerekayo alipire ndithu choŵetacho. Koma ngati chili kwa mwiniwakeyo, wobwereka uja asalipire. Choŵetacho akachibwereka, tsono nkuwonongeka, mtengo wolipira pobwereka ndiwo udzakonze mlanduwo. “Munthu akanyenga namwali wosadziŵa mwamuna, yemwe sanatomeredwe, nagona naye, alipire chiwongo, ndipo amkwatire. Koma ngati bambo wake wa namwaliyo akana kuti mwana wakeyo asakwatiwe, munthuyo adzangolipirabe ndalama za chiwongo cha namwali. “Munthu wamkazi wochita zaufiti, musamlole kuti akhale moyo. “Aliyense wogona ndi nyama aphedwe basi. “Aliyense wopereka nsembe kwa milungu, osati kwa Chauta yekha, aphedwe ameneyo. “Musazunze mlendo kapena kumkhalitsa m'phanthi, poti paja inunso munali alendo ku dziko la Ejipito. Musazunze mkazi wamasiye kapena mwana wamasiye. Mukamaŵazunza, Ine ndidzaŵamva iwowo akamalira kwa Ine. Ndidzakukwiyirani, ndipo ndidzakuphani ku nkhondo. Akazi anu adzasanduka amasiye, ndipo ana anunso adzasanduka amasiye. “Mukakongoza ndalama munthu wina aliyense waumphaŵi pakati panupo, musamachita monga momwe amachitira anthu okongoza, musamuumirize kupereka chiwongoladzanja. Mukatenga mwinjiro wa munthu wina ngati chigwiriro kuti adzakulipireni, muubweze dzuŵa lisanaloŵe, poti chofunda nchokhacho, ndicho chotetezera thupi lake. Nanga adzafunda chiyani? Akalira kwa Ine iyeyu kuti ndimthandize, ndidzamuyankha chifukwa ndine wachifundo. “Musanyoze Mulungu, ndipo musatemberere mtsogoleri wa anthu anu. “Musachedwe kundipatsa zopereka zotapa pa zokolola zanu zambiri ndiponso pa vinyo wanu wochuluka. “Mundipatse ana anu achisamba aamuna. Mundipatsenso ana oyamba kubadwa a ng'ombe zanu ndi nkhosa zanu. Mwana woyamba kubadwayo adzangokhala ndi mai wake masiku asanu ndi aŵiri, ndipo mudzampereka kwa Ine pa tsiku lachisanu ndi chitatu. “Mudzakhale anthu operekedwa kwa Ine. Motero musadzadye nyama ya choŵeta chilichonse chojiwa ndi zilombo ku thengo. Nyama imeneyo mudzapatse agalu. “Usachite umboni wonama. Munthu wolakwa usamthandize pakumchitira umboni wonama. Ngakhale anthu ambiri akamachita choipa, usamavomerezana nawo. Ndipo usamapereka umboni wopotoza chiweruzo m'bwalo lamilandu, kuti ukondweretse anthu ambiri. Munthu wosauka ukamuweruza, usaweruze mokondera. “Ukaona ng'ombe ya mdani wako ikusokera, kapena bulu wake, utenge ukampatse. Bulu wa mdani wako akagwa ndi katundu, usabzole ndi kumsiya, koma umthandize kuti adzuke. “Ngati mmodzi mwa anthu ako osauka aimbidwa mlandu, umuweruze molungama ndithu. Ulewe zabodza, zosinjirira. Usaphe munthu wosalakwa ndi wosapalamula, chifukwa Ine sindidzakhululukira wochimwa. Usalandire chiphuphu poti chimadetsa m'maso anthu oweruza, ndipo motero mlandu umaipira anthu osalakwa. “Musazunze mlendo. Inu nomwe mukudziŵa m'mene amamvera mlendo, poti paja inunso munali alendo ku Ejipito kuja. “Muzibzala mbeu zaka zisanu ndi chimodzi m'munda mwanu, ndi kumakolola mbeuzo. Koma chaka chachisanu ndi chiŵiri mudzaipumuze mindayo. Anthu osauka a mtundu wanu ndiwo adzadye zomera m'mindamo, ndipo nyama zakuthengo zidzadya zotsala. Muzidzachita chimodzimodzi ndi minda yamphesa ndi yaolivi yomwe. “Muzigwira ntchito masiku asanu ndi limodzi, koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri musamagwira ntchito, kuti ng'ombe zanu zipume pamodzi ndi abulu anu omwe, kutinso akapolo anu ndi alendo omwe apezenso mphamvu. Mumvetse zonse zimene ndakuuzanizi. Musamapemphera kwa milungu ina, ndi maina ake omwe musamaŵatchula. “Muzikhala ndi tsiku lachikondwerero katatu pa chaka, kuti mundilemekeze Ine. Muzikhala ndi tsiku la chikondwerero cha Buledi Wosatupitsa. Monga ndidakulamulirani, muzidya Buledi Wosatupitsa masiku asanu ndi aŵiri pa mwezi wa Abibu, pa nthaŵi yake, chifukwa mudatuluka ku Ejipito mwezi umenewo. Munthu asadzaonekere pamaso panga ali chimanjamanja. Muzikhalanso ndi tsiku la chikondwerero cha Masika pokolola mbeu zoyamba zochokera ku zobzala zanu. Muzikhalanso ndi tsiku la chikondwerero cha kututa zokolola zonse pakutha pa chaka, pamene muika m'nkhokwe dzinthu dzanu dzonse. Anthu aamuna onse aziwonekera pamaso pa Ine Chauta pa masiku atatu ameneŵa. “Mukamapereka magazi a nyama ngati nsembe kwa Ine, musapereke pamodzi ndi buledi wofufumitsa, ndipo mafuta a nyama yopereka pa tsiku langa lachikondwerero asakhale mpaka m'maŵa. “Muzibwera ndi zokolola zoyamba zabwino kwambiri za kumunda kwanu ku Nyumba ya Chauta, Mulungu wanu. “Musamaphika kamwanakanyama mu mkaka wa make. “Ndikutuma mngelo wanga patsogolo panu, kuti akutchinjirizeni pa njira ndi kukufikitsani ku malo amene ndakukonzerani. Mumvere iyeyo, ndipo mumvetse zimene akunena. Musamchite zaupandu, chifukwa sadzakhululukira tchimo lotere. Iye akuchita zimenezi m'dzina langa. Koma mukamvera iyeyo ndi kuchita zonse zimene ndinena, Ineyo ndidzadana ndi adani anu, ndipo onse amene atsutsana nanu ndidzalimbana nawo. “Mngelo wanga adzapita patsogolo panu, ndipo adzakuloŵetsani m'dziko la Aamori, Ahiti, Aperizi, Akanani, Ahivi ndi Ayebusi, ndipo ndidzaŵaononga onsewo. Tsono musagwadire milungu yao kapena kuipembedza. Musamachita nao zimene amachita anthu amenewo. Mukaonongeretu milungu yao, ndiponso mukaphwanye miyala yao yopembedzerapo. Muzipembedza Chauta, Mulungu wanu, tsono ndidzakudalitsani pokupatsani chakudya ndi madzi, ndipo ndidzakuchiritsani matenda onse. Palibe mkazi amene adzapititse padera m'dziko mwanumo, ndipo wosabala sadzaoneka. Ndidzakupatsani moyo wautali. Anthu onse olimbana nanu ndidzaŵachititsa mantha kuti andiwope Ine. Ndidzadzetsa chisokonezo pakati pa anthu amene mukumenyana nawo. Ndipo adani anu onse ndidzaŵathamangitsa liŵiro lamtondowadooka. Ndidzapirikitsa Ahivi, Akanani ndi Ahiti, inu musanafike, ndipo adzathaŵa monga ngati ndaŵatumira mavu. Sindidzaŵapirikitsa chaka chimodzinchimodzi, kuti dzikolo lingadzakhale lopanda anthu ndi kukusiyirani nyama zakuthengo zokhazokha. Koma ndidzaŵapirikitsa pang'onopang'ono, mpaka mutabala ana ambiri amene angathe kutenga dzikolo, kuyambira ku Nyanja Yofiira mpaka ku Nyanja Yaikulu ya Afilisti, ndi kuyambiranso ku chipululu mpaka ku mtsinje wa Yufurate. Ndidzakupatsani mphamvu zopambanira anthu a m'dzikolo, ndipo mudzaŵapirikitsa. Musadzachite nawo chipangano iwowo kapenanso milungu yao. Asadzakhale m'dziko mwanu, kuwopa kuti angadzakuchimwitseni. Mukamapembedza milungu yao, ndithu mudzakodwa mu msampha.” Mulungu adauza Mose kuti, “Bwera kwa Ine kuno ku phiri pamodzi ndi Aroni, Nadabu, Abihu ndiponso atsogoleri a Aisraele 70. Tsono mundipembedze Ine muli chapatali ndithu. Mose yekha ndiye andiyandikire, koma enawo asafike pafupi. Anthu ena onse nawonso asabwere ndi Moseyo.” Mose adapita kukauza anthu mau ndi malangizo onse amene Chauta adamuuza. Ndipo anthu onse adayankha kuti, “Tidzachita zonse zimene Chauta wanena.” Apo Mose adalemba mau onse a Chauta. Ndipo adadzuka m'maŵa ndithu nayamba kumanga guwa patsinde pa phiri. Kenaka adaimiritsa miyala khumi ndi iŵiri ya mafuko khumi ndi aŵiri a Aisraele. Tsono adatuma Aisraele achinyamata kuti iwoŵa apereke nsembe zopsereza, ndi kupha ng'ombe kuti apereke nsembe zamtendere kwa Chauta. Mose adatengako theka la magazi, naŵathira m'mbale, ndipo magazi otsala adawaza pa guwa. Pambuyo pake adatenga buku lachipangano, naŵaŵerengera momveka anthuwo. Tsono anthuwo adati, “Tidzachita zonse zimene Chauta walamula. Tidzamumvera Iyeyo.” Apo Mose adatenga magazi am'mbale aja, nawaza anthuwo, ndipo adati, “Magazi ameneŵa ndiwo amene akutsimikiza chipangano chimene Chauta wapangana nanu pakukupatsani mau onseŵa.” Tsono Mose, Aroni, Nadabu ndi Abihu ndiponso anthu 70 mwa atsogoleri aja a Aisraele, adakwera phiri, ndipo adaonana ndi Mulungu wa Aisraele. Pansi pa mapazi ake panali china chooneka ngati mseu wopangidwa ndi mwala wa safiro woyalidwa bwino, wa maonekedwe onga thambo. Mulungu sadaŵaononge atsogoleri a Aisraelewo. Iwowo adampenyadi Mulungu, kenaka adadya ndi kumwa. Chauta adauza Mose kuti, “Bwera kwa Ine kuphiri kuno, ndipo udikire konkuno. Ndidzakupatsa miyala imene ndalembapo malamulo, kuti ndiphunzitse anthu.” Apo Mose adanyamuka pamodzi ndi mtumiki wake Yoswa, ndipo Moseyo adakwera phiri la Mulungu. Iyeyo anali atauza atsogoleri aja kuti, “Batiyembekezani pano, mpaka tidzakupezeni. Aroni ndi Huri muli nawo pompano. Amene akhale ndi milandu, apite kwa iwowo.” Tsono Mose adakwera phiri, ndipo phirilo lidaphimbidwa ndi mtambo. Ulemerero wa Chauta udatsikira pa phiri la Sinai, ndipo lidaphimbidwa ndi mtambo masiku asanu ndi limodzi. Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri Chauta adaitana Mose m'kati mwa mtambomo. Kwa Aisraele aja, ulemerero wa Chauta uja unkaoneka ngati malaŵi a moto pa phiri. Mose adakaloŵa mumtambomo mpaka kukafika pamwamba pa phiri. Adakhala kumeneko masiku makumi anai, usana ndi usiku. Chauta adauza Mose kuti, “Uza Aisraele apereke zopereka zao kwa Ine. Tsono iwe ulandire zoperekazo kwa munthu aliyense wa mtima wofuna kupereka. Zopereka zimene ulandirezo ndi izi: golide, siliva, mkuŵa, nsalu zobiriŵira, zofiirira ndi zofiira, nsalu zokoma zathonje, nsalu zopangidwa ndi ubweya wambuzi, zikopa zankhosa zonyika mu utoto wofiira, zikopa zofeŵa, matabwa a mtengo wa kasiya, mafuta a nyale, zonunkhira za mafuta odzozera, ndiponso lubani wa fungo lokoma. Ulandirenso miyala yokoma ya onikisi, ndiponso miyala ina yoti uike pa chovala chaunsembe cha efodi, ndi pa chovala chapachifuwa. Ndipo andipangire chihema chopatulika kuti Ine ndidzakhale pakati pao. Umange chihemacho monga m'mene ndidzakulangizire mapangidwe ake ndiponso mapangidwe a katundu yense wam'menemo. “Ndipo apange bokosi la matabwa a mtengo wa kasiya. Kutalika kwake kukhale masentimita 114, muufupi mwake masentimita 69, msinkhu wake masentimita 69. Ulikute ndi golide wabwino kwambiri m'kati mwake ndi kunja komwe. Upange mkombero wagolide kuzungulira bokosi lonselo. Upange mphete zinai zagolide zonyamulira bokosilo, ndi kumangirira mphetezo ku miyendo yake inai, uku ziŵiri uku ziŵiri. Upangenso mphiko zakasiya, ndipo mphikozo uzikute ndi golide. Mphiko zimenezo udzazilonge m'mphetezo pa mbali ziŵiri za bokosilo, kuti azinyamulira. Mphikozo zidzangokhala m'mphetezo osazitulutsanso. M'bokosimo udzaikemo miyala iŵiri yolembedwapo Malamulo imene ndidzakupatse. “Upange ndi golide wabwino kwambiri chivundikiro cha bokosi, kutalika kwake masentimita 114, kupingasa kwake masentimita 69. Pa mbali ziŵiri za chivundikirocho, m'mphepete mwake, upange akerubi aŵiri, agolide, osula ndi nyundo, wina uku wina uku. Akerubiwo uŵalumikize ndi chivundikiro. Mapiko a akerubiwo adzatambasukire pamwamba pa chivundikirocho, kuti adzachiphimbe. Akerubi adzakhale choyang'anana, aliyense kumayang'ana chivundikirocho. Chivundikiro cha bokosicho udzachiike pamwamba pa bokosilo, ndipo m'bokosimo udzaikemo miyala iŵiri ija ya Malamulo imene ndidzakupatse. Ndizidzakumana nawe kumeneko, ndipo kuchokera pamwamba pa chivundikirocho, pakati pa akerubi ali pamwamba pa bokosiwo, ndidzakuuza malamulo okhudza anthu anga Aisraele. “Upange tebulo la matabwa a mtengo wa kasiya, kutalika kwake masentimita 91, muufupi mwake masentimita 46, msinkhu wake masentimita 69. Tsono ulikute ndi golide wabwino kwambiri ndipo pozungulira pake ponse upange mkombero wagolide. Upange fulemu lozungulira tebulo, muufupi mwake kuyesa chikhatho, ndipo upange mkombero wagolide wozungulira fulemulo. Upange mphete zinai zagolide, ndipo uzilumikize ku ngodya zinai za ku miyendo yake inai. Mphete zopisamo mphiko zonyamulira tebulolo ziikidwe pafupi ndi fulemu lija. Upange mphiko zonyamulira za mtengo wa kasiya, ndipo uzikute ndi golide. Upange mbale ndi zipande zofunika popereka lubani, ndiponso mitsuko ndi mabeseni ofunika pa zopereka za chakumwa. Zonsezi zikhale za golide wabwino kwambiri. Patebulopo uziikapo buledi woperekedwa kosalekeza, kuti azikhala pamaso panga nthaŵi zonse. “Upange choikaponyale cha golide wabwino kwambiri. Tsinde lake ndi thunthu lake zikhale zagolide, ndipo uchisule ndi nyundo. Zikho zake, ndiye kuti nkhunje ndi maluŵa ake, zonsezo zipangidwire kumodzi. Pa mbali zake pakhale mphanda zisanu ndi imodzi, zitatu pa mbali iliyonse. Mphanda yoyamba ikhale ndi zikho zitatu zopangidwa ngati maluŵa amtowo, nkhunje ndi duŵa. Ku mphanda ina kukhalenso zikho zitatu zonga maluŵa amtowo, nkhunje ndi duŵa. Zikhale momwemo mphanda zonse zisanu ndi imodzi zotuluka m'choikaponyalecho. Pa choikaponyalecho padzakhale maluŵa anai a maonekedwe onga maluŵa amtowo, okhala ndi nkhunje ndi maluŵa ake. Padzakhale nkhunje imodzi m'munsi mwake mwa magulu atatu a mphanda zija, utazipatula ziŵiriziŵiri. Nkhunjezo pamodzi ndi mphandazo zidzapangidwire kumodzi ndi choikaponyalecho. Chonsecho chidzangokhala chimodzi, chopangidwa ndi golide, chosula ndi nyundo. Upange nyale zisanu ndi ziŵiri, ndipo uziike pa choikaponyale chija, kuti ziziwunikira kutsogolo. Mbano zogwirira, pamodzi ndi timbale take tomwe, zikhale za golide wabwino kwambiri. Choikaponyalecho ndi zipangizo zonse uzipange ndi golide wolemera makilogaramu 34. Usamale kuti upange zimenezi monga momwe ndikukuwonetsera paphiri pano. “Upange chihema chamapemphero ndi nsalu khumi za bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, ndiponso ndi nsalu zobiriŵira, zofiirira ndi zofiira. Nsalu zimenezi uzipete bwino ndi zithunzi za akerubi. Muutali nsalu iliyonse ikhale mamita 13, ndipo muufupi mwake ikhale pafupi mamita aŵiri. Zonsezo zikhale zofanana. Usoke nsalu zisanu kuti zikhale nsalu imodzi, ndipo uchitenso chimodzimodzi ndi nsalu zisanu zinazo. Upange timagonga ta nsalu yobiriŵira m'mbali mwake mwa nsalu imodzi kumapeto kwake. Uchitenso chimodzimodzi ndi nsalu inzakeyo. Kenaka upange timagonga makumi asanu pa nsalu yoyambayo, ndipo timagonga tinanso makumi asanu pa nsalu yachiŵiriyo, kuti timagongato tiyang'anane. Tsono upange ngoŵe zagolide makumi asanu, zolumikizira nsalu ziŵirizo, kuti chipangike chihema chimodzi. “Uwombenso nsalu khumi ndi imodzi za ubweya wambuzi kuti zikhale lona lophimba pamwamba pa chihemacho. Muutali mwake nsalu iliyonse ikhale mamita 14, ndipo muufupi mwake pafupi mamita aŵiri. Zonsezo zikhale zofanana. Usoke nsalu zisanu kuti zikhale nsalu imodzi, ndipo zisanu ndi imodzi zinazo zikhalenso nsalu imodzi. Tsono upinde nsalu yachisanu ndi chimodziyo mophatikiza patsogolo pa chihema. Upangenso magonga makumi asanu m'mbali mwake mwa nsalu yotsirizira ya chinsalu chimodzi, ndiponso magonga makumi asanu pa nsalu yotsiriza inayo. “Upange zomangira makumi asanu zamkuŵa, ndipo uziike m'magongamo. Choncho uphatikize pamodzi nsalu ziŵirizo, kuti pakhale chihema chimodzi. Theka la nsalu yotsalira ija idzalendeŵera kumbuyo kwa chihemacho. “Ndipo nsalu ya masentimita 46 yotsalira m'litali mwake pa mbali ziŵiri, izidzalendeŵera ndi kuphimba mbali ziŵirizo. Lona lija ulipangire chophimbira chake chofiira cha chikopa cha nkhosa zamphongo. Pambuyo pake upangenso chophimbira chotsiriza cha zikopa zofeŵa chodzayala pamwamba pa zonse. “Upange mafulemu a chihemacho ndi matabwa oimirira bwino a mtengo wa kasiya. Muutali mwake fulemu lililonse likhale mamita anai ndi theka, ndipo muufupi mwake masentimita 69. Thabwa lililonse likhale ndi zolumikizira ziŵiri, ndipo mafulemu onse a chihemacho apangidwe ndi matabwa otere. Popanga mafulemuwo, ku mbali yakumwera, upange makumi aŵiri. Ndipo upange masinde makumi anai asiliva pansi pa mafulemu makumi aŵiriwo. Pansi pa fulemu lililonse pakhale masinde aŵiri ogwirizira zolumikizira ziŵiri zija. Ndipo kumpoto kwa chihemacho upangenso mafulemu makumi aŵiri, ndi masinde makumi anai asiliva, aŵiri pa fulemu lililonse. Kumbuyo kwake kwa chihemacho, chakuzambwe, upange mafulemu asanu ndi limodzi. Kumbuyo kwa chihema konko, pangodya pakhale mafulemu aŵiri. Mafulemu ameneŵa apangodya azilumikizidwa kuyambira pansi mpaka pa chigwinjiri chapamwamba. Umu ndimo m'mene akhalire mafulemu aŵiri amene akupanga ngodya ziŵiri. Motero padzakhala mafulemu asanu ndi atatu okhala ndi masinde ake 16 asiliva, aŵiri pansi pa fulemu lililonse. “Upange mitanda ya mtengo wa kasiya, isanu pa mafulemu a mbali ina ya chihema, ndi isanu inanso pa mafulemu a mbali ina. Pakhalenso mitanda isanu pa mafulemu akuzambwe chakumbuyo. Mtanda wa pakati penipeni pa mafulemuwo ugwire mafulemu onse, kuyambira ku mapeto mpaka ku mapeto. Mafulemuwo uŵakute ndi golide, ndi kulonganso mphete zagolide m'mafulemuwo kuti agwirizire mitanda ija, ndipo mitandayo ikhale yokutidwa ndi golide. Motero upange chihema changa monga momwe ndikukulangizira paphiri pano. “Usoke nsalu yotchingira yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino. Ndipo nsaluyo uipete ndi zithunzi za akerubi. Uikoloŵeke pa nsanamira zinai zakasiya zokutidwa ndi golide, zokhala ndi ngoŵe zagolide ndi zokhazikika pa masinde anai asiliva. Ukoloŵeke nsalu yochingayo ku ngoŵezo ndipo uike bokosi lachipangano lija m'kati momwemo, kuseri kwa nsalu yochingayo. Nsalu yochingayo idzalekanitsa malo opatulika ndi malo opatulika kopambana. Uike chivundikiro chija pa bokosi lachipangano ku malo opatulika kopambanawo. Tebulo lija uliike kunja kwa nsalu yochingayo. Choikaponyale chija uchiike chakumwera kwake kwa chihemacho, mopenyana ndi tebulolo, limene likhale mbali yakumpoto. “Pa chipata choloŵera m'chihemamo, uikepo nsalu yochingira yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndi ya bafuta wosalala, wopikidwa bwino ndi wopetedwa mwaluso. Upange nsanamira zisanu zakasiya zimene akoloŵekepo nsalu yochingayo. Zikutidwe ndi golide, ndipo ngoŵe zake zokoloŵekapo zikhalenso zagolide, ndiponso upange masinde asanu amkuŵa a nsanamira zimenezo. “Upange guwa la nsembe zopsereza la matabwa a mtengo wa kasiya. Likhale lalibanda: muutali mwake likhale masentimita 229, muufupi mwake chimodzimodzi: masentimita 229, msinkhu wake masentimita 137. Upange nyanga pa ngodya zake zinaizo, zilumikizane ndi guwalo, ndipo ulikute ndi mkuŵa. Upangenso mbale zake zolandirira phulusa, mafosholo, mabeseni, mafoloko aakulu ndiponso ziŵiya zosonkhapo moto. Zipangizo zonse za ku guwalo zikhale zamkuŵa. Upangenso chitsulo chamkuŵa choboolaboola ngati sefa. Pa ngodya zake za chitsulocho upange mphete zamkuŵa zonyamulira. Uike sefayo m'munsi mwake mwa chibumi cha guwalo, ndipo ilekeze pakati pa guwalo. Upange mphiko ya mtengo wa kasiya yonyamulira guwalo, ndipo uikute ndi mkuŵa. Ponyamula guwalo, mphikozo azizipisa m'mphete za pa mbali ziŵiri za guwalo. Ndipo guwalo udzalipange mogoba m'kati mwake. Ulipange monga momwe ndikukulangizira paphiri pano. “Pambuyo pake upange bwalo la chihema, lochingidwa. Chakumwera kwake kukhale nsalu zochinga za bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, kutalika kwa mbali imodzi kukhale mamita 46. Nsanamira zake 20 ndi masinde ake 20 zikhale zamkuŵa, koma ngoŵe za nsanamirazo, pamodzi ndi mitanda yake, zikhale zasiliva. Momwemonso pa mbali yakumpoto, uike nsalu zochinga, kutalika kwake mamita 46, ndi nsanamira zamkuŵa makumi aŵiri. Nsanamirazo zimangidwe pa masinde ake makumi aŵiri, koma ngoŵe za nsanamirazo ndi mitanda yake zikhale zasiliva. Muufupi mwake mwa bwalolo cha mbali yakuzambwe, pakhale nsalu zochinga, kutalika kwake mamita 23, ndi nsanamira khumi ndi masinde khumi. Chakuvuma, komwe kuli chipata chake, bwalolo likhalenso mamita 23 muufupi mwake. Pa mbali ina ya chipata pakhale nsalu zochinga, kutalika kwake mamita asanu ndi aŵiri, ndi nsanamira zitatu ndi masinde atatu. Chimodzimodzi pa mbali ina pakhalenso nsalu zochinga, kutalika kwake mamita asanu ndi aŵiri, ndi nsanamira zitatu ndi masinde atatu. Pa chipata cha bwalolo pakhale nsalu yochinga yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndi ya bafuta wosalala, wopikidwa bwino ndi wopetedwa mwaluso. Kutalika kwake kukhale mamita asanu ndi anai. Ikhale ndi nsanamira zinai zomangidwa pa masinde anai. Nsanamira zonse kuzungulira bwalolo zilumikizidwe ndi mitanda yasiliva, ndipo ngoŵe zake zikhalenso zasiliva, koma masinde ake akhale amkuŵa. Kutalika kwake kwa bwalolo kukhale mamita 46, muufupi mwake mamita 23, msinkhu wake masentimita 230. Nsalu zochingazo zikhale za thonje losankhidwa bwino kwambiri ndi lopikidwa, ndipo masinde ake akhale amkuŵa. Zipangizo zonse zogwiritsira ntchito zosiyanasiyana m'chihemamo, pamodzi ndi zikhomo za chihemacho ndi za bwalolo, zonsezo zikhale zamkuŵa. “Uŵalamule Aisraele kuti akupatse mafuta aolivi opsinyidwa bwino, oyatsira nyale, kuti ziziyaka kosalekeza. Aroni ndi ana ake aamuna aziyatsa nyale m'chihema chamsonkhanomo amakumana ndi anthu ake, kunja kwa chochinga, patsogolo pa miyala yaumboni ija. Tsono nyalezo ziziyaka kumeneko kuyambira madzulo mpaka m'maŵa. Lamulo limeneli adzalisunge Aisraele ndi zidzukulu zao mpaka muyaya. “Aroni ndi ana ake aamuna apatulidwe pakati pa Aisraele ndipo abwere kwa iwe, kuti akhale ansembe onditumikira. Abwere Aroni pamodzi ndi ana ake Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara. Umsokere mkulu wako Aroni zovala zopatulika, kuti aziwoneka wolemerera ndi wolemekezeka. Ulamule anthu onse aluso, onse amene ndaŵapatsa nzeru, kuti asoke zovala za Aroni zozivala pamene udzampatule kuti akhale wansembe wanga. Zovala zimene udzasokezo ndi izi: chovala chapachifuwa, chovala cha efodi, mkanjo, mwinjiro wopetedwa bwino, nduŵira ndi lamba. Asoke zovala zopatulikazo za mbale wako Aroni ndi za ana ake, kuti akhale ansembe onditumikira. Zovala zimenezi anthu alusowo azisoke ndi nsalu yagolide, ndi nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino. Efodi aisoke ndi nsalu yagolide, ndi nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso ya bafuta wosalala, wopikidwa bwino ndi wopetedwa mwaluso. Idzakhale ndi tizikwewo tam'mapewa tiŵiri tosokerera ku nsonga zake ziŵiri, tomangira efodiyo. Padzakhalenso lamba woluka mwaluso, womangira efodi, wolukira kumodzi ndi efodiyo. Lambayo nayenso adzakhale wa nsalu ya golide, ndi wa nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino. Utenge miyala iŵiri ya onikisi, ndipo ulembepo maina a ana a Israele. Pa mwala umodzi ulembepo maina asanu ndi limodzi, ndipo pa mwala winawo uchitenso chimodzimodzi. Ulembe mainawo motsatana malinga nkubadwa kwa ana a Israelewo. Maina aowo uŵalembe mozokota pa miyala iŵiriyo, potsata luso la mmisiri wozokota miyala. Ndipo miyalayo uiike m'zoikamo zake zagolide. Uike miyala iŵiri imeneyi pa tizikwewo tam'mapewa ta efodi, ngati chikumbutso cha ana a Israele. Mwa njira imeneyi, Aroniyo azidzanyamula pa mapewa mainawo, ndipo Chauta azidzaŵakumbukira iwowo. Upangenso zoikamo zonga maluŵa agolide, ndiponso maunyolo aŵiri a golide wokoma, opotedwa ngati zingwe, amene udzaŵalumikize ku zoikamozo. “Tsono usoke chovala chapachifuwa, chopetedwa mwaluso, chomavala poweruza. Mapangidwe ake akhale ngati a efodi, ndiye kuti a nsalu yagolide, ndi nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino. Kukula kwake kukhale kofanana mbali zonse, ndipo chikhale chopinda paŵiri. M'litali mwake chikhale masentimita 23, muufupi mwake chimodzimodzi. Usokererepo mizere inai ya miyala. Pa mzere woyamba pakhale miyala ya rubi, topazi ndi garaneti. Pa mzere wachiŵiri pakhale miyala ya emeradi, safiro ndi daimondi. Pa mzere wachitatu pakhale miyala ya yasinti, agate ndi ametisiti. Pa mzere wachinai pakhale miyala ya berili, onikisi ndi jasipere, ndipo zonsezo ziikidwe m'zoikamo zagolide. Miyala imeneyi ikhalepo khumi ndi iŵiri, potsata maina a mafuko a Aisraele. Miyalayo izokotedwe ngati zidindo, uliwonse ukhale ndi dzina la fuko limodzi. Upange timaunyolo ta golide wabwino kwambiri ta pa chovala chapachifuwa, topota mwaluso ngati maukufu. Upangenso mphete ziŵiri, ndipo uzilumikize pa ngodya zam'mwamba za chovala chapachifuwa. Umange zingwe zagolide ziŵiri ku mphete ziŵirizo. Ndipo nsonga zake zina ziŵiri za zingwezo uzimange ku zoikamo zake zija. Upangenso mphete ziŵiri zagolide, ndipo uzilumikize ku ngodya zam'munsi za chovala chapachifuwa, ku nsonga yake yam'kati, pafupi ndi chovala cha efodi chija. Upangenso mphete zina ziŵiri zagolide, ndipo uzilumikize cham'munsi, kutsogolo kwake kwa malamba aŵiri a pa mapewa a efodi, pafupi ndi misoko, pa lamba wolukidwa mwaluso uja. Tsono ulumikize mphete za chovala chapachifuwacho ku mphete za chovala cha efodi chija ndi kamkuzi kobiriŵira, kuti chovala chapachifuwacho chikhale pamwamba pa lamba wolukidwa mwaluso uja, ndipo chovala chapachifuwa chilumikizike bwino ku chovala cha efodi. Ndipo Aroni akamaloŵa m'malo opatulika, azivala chovala chapachifuwa cholembedwa maina onse a ana a Israele, kuti Chauta azidzaŵakumbukira. M'chovala chapachifuwacho uziikamo zinthu zoyera za Chauta zotchedwa Urimu ndi Tumimu, kuti zimenezo zikhale pa chifuwa cha Aroni akamapita kwa Chauta. Motero Aroni akakhala pamaso pa Chauta, nthaŵi zonse adzakhala ndi zomthandiza kuweruza bwino mpingo wa Israele. “Upange mkanjo wa nsalu yobiriŵira, wophimba chovala cha efodi chija. Pakati pake pa mkanjowo usiye chiboo chopisapo mutu. Chiboo chimenechi chikhale chosokerera mwamphamvu mozungulira monse, ngati khosi la malaya, kuti mkanjowu usang'ambike. Pa mpendero wapansi wa mkanjowo, upange zinthu zonga makangaza. Zikhale za thonje lobiriŵira, lofiirira ndi lofiira, kuzungulira mkanjo wonsewo. Pakati pa makangazawo pakhale timabelu tagolide. Choncho pakhale khangaza limodzi ndi kabelu kamodzi, khangaza limodzi ndi kabelu kamodzi, kuzungulira mpendero wonse wam'munsiwo. Tsono Aroni azivala mkanjowo pamene akutumikira zaunsembe. Akamaloŵa m'malo opatulika pamaso pa Chauta kapena pochoka kumeneko, liwu la timabeluto lizidzamveka, kuti asafe. “Upangenso duŵa la golide wabwino kwambiri, ulembepo mozokota mau akuti, ‘Choperekedwa kwa Chauta.’ Ulimange ndi kamkuzi kobiriŵira pa nduŵira ya Aroni, ndipo likhale cha kutsogolo kwa nduŵirayo. Likhaledi pamphumi pake pa Aroni, motero asenze iye yemwe cholakwa chilichonse cha pa zopereka zimene Aisraele amazipatulira Chauta. Kuti Chauta alandire zopereka za anthuzo, Aroni azivala duŵali pa nduŵira yake nthaŵi zonse. “Umsokerenso Aroni mwinjiro wa bafuta wokoma, ndipo umpangire nduŵira ya bafuta wokoma, ndiponso lamba wopetedwa mokongola. “Ana a Aroni, uŵasokere miinjiro, malamba ndi nduŵira, kuti azisiyana ndi anthu ena, ndipo iwowo aziwoneka olemerera ndi olemekezeka. Zovala zimenezi uveke mbale wako Aroni ndi ana ake. Tsono uŵadzoze, uŵapatse udindo ndi kuŵapatula, kuti akhale ansembe onditumikira. Uŵasokere akabudula ofika m'ntchafu, kuti asamaonetse maliseche. Aroni ndi ana ake azivala zimenezi nthaŵi zonse akamapita ku chihema chamsonkhano kapena ku guwa, kukanditumikira ku malo opatulika aja, kuwopa kuti angachimwe ndipo angafe. Lamulo limeneli, lonena za Aroni ndi zidzukulu zake, ndi lokhazikika mpaka muyaya. “Pofuna kumpatula Aroni ndi ana ake, kuti akhale ansembe onditumikira, uchite izi: Utenge ng'ombe yamphongo ndi nkhosa zamphongo ziŵiri zopanda chilema. Utengenso buledi wosafufumitsa, makeke osatupitsa, osakaniza ndi mafuta, ndiponso mitanda ya buledi yopsapsalala yopaka mafuta. Zimenezi uzipange ndi ufa wosalala watirigu. Uziike m'lichero, ndipo ubwere nazo kwa Ine, pamene ukupereka nsembe ng'ombe yamphongo ija ndi nkhosa zija. Ubwere naye Aroni ku khomo la chihema chamsonkhano, pamodzi ndi ana ake aamuna, ndipo onsewo uŵayeretse m'madzi. Tsono utenge zovala zija ndi kumuveka Aroni mwinjiro ndi mkanjo wautali wovala pamwamba pa efodi, ndiponso chovala chapachifuwa. Ndipo umange lamba woluka mwaluso uja m'chiwuno mwake. Umuveke nduŵira kumutu kwake, ndi duŵa lopatulika lija panduŵirapo. Tsono utenge mafuta odzozera aja ndi kuŵatsanyulira kumutu kwake kuti umdzoze. Kenaka ubwere ndi ana ake aamuna, ndipo uŵaveke miinjiro. Uŵavekenso lamba m'chiwuno mwao ndi nduŵira. Motero iwoŵa adzakhala ansembe anga potsata lamulo langa losatha. Umu ndimo m'mene umdzozere Aroni ndi ana ake aamuna. “Pambuyo pake ubwere ndi ng'ombe yamphongo pakhomo pa chihema chamsonkhano. Tsono Aroni ndi ana ake asanjike manja ao pamutu pa ng'ombeyo. Kenaka muiphe ng'ombeyo pamaso pa Chauta, pa khomo la chihema chamsonkhano. Utengeko magazi a ng'ombeyo, ndipo uŵapake ndi chala chako pa nyanga za guwa. Tsono magazi otsalawo uŵatsanyulire patsinde pa guwalo. Pambuyo pake utenge mafuta onse okuta matumbo, mphumphu ya mafuta akuchiŵindi, ndiponso imso ziŵiri, pamodzi ndi mafuta ozikuta. Zonsezi uzipereke, ndipo uzitenthere pa guwalo. Koma nyama yake, chikumba chake ndi ndoŵe zake, ukazitenthere kunja kwa mahema. Chopereka chimenechi ndicho cha nsembe yopepesera machimo. “Utenge imodzi mwa nkhosa ziŵiri zamphongo zija, ndipo Aroni ndi ana ake aamuna asanjike manja ao pamutu pa nkhosayo. Tsono uiphe ndipo utenge magazi ake ndi kuwaza pa mbali zonse za guwa. Nkhosayo uiduledule, ndipo utatsuka matumbo ndi miyendo yake, uziike mosanjikiza pamwamba pa nthuli zake ndi mutu. Ndipo upsereze nkhosa yonseyo paguwapo. Imeneyo idzakhala nsembe yopsereza yopereka kwa Chauta. Idzakhala nsembe ya fungo lokoma yopereka pa moto kwa Chauta. “Tsono utenge nkhosa yamphongo inayo. Aroni ndi ana ake aamuna asanjike manja ao pamutu pa nkhosayo. Muiphe, ndipo mutengeko magazi ake ndi kupaka pa khutu la ku dzanja lamanja la Aroni, ndi pa khutu la ku dzanja lamanja la ana ake aamuna. Upakenso pa chala chao chachikulu cha ku dzanja lamanja, ndi pa chala chachikulu cha ku phazi la ku dzanja lamanja. Magazi ena uwaze pa mbali zonse za guwa. Utengeko magazi otsalira pa guwa ndiponso mafuta ena odzozera, uwaze Aroni ndi zovala zake. Uwazenso ana ake ndi zovala zao. Tsono iyeyo ndi ana ake adzakhala opatulika, pamodzi ndi zovala zomwezo. “Nkhosa yamphongo ija utengeko mafuta ake, mchira wake wamafuta, mafuta okuta matumbo, mphumphu ya mafuta akuchiŵindi, imso ziŵiri ndi mafuta ozikutawo, ndiponso ntchafu ya ku dzanja lamanja, chifukwa nkhosa imeneyi ndi nsembe ya pa mwambo wodzozera. M'lichero limene lili m'Nyumba ya Chauta utengeko buledi mmodzi wosafufumitsa, keke imodzi yosakaniza ndi mafuta, ndiponso buledi mmodzi wopsapsalala. Chakudya chonsechi uchiike m'manja mwa Aroni ndi mwa ana ake, ndipo iwowo achiweyule kuti chikhale chopereka choweyula kwa ine. Kenaka uchotse zonsezo m'manja mwao, ndipo uzipsereze pa guwa, pamwamba penipeni pa zopereka zija kuti zipereke fungo lokondweretsa Chauta. Imeneyi ndiyo nsembe yopsereza kwa Chauta. “Utenge nganga ya nkhosa yamphongo imene adaipha podzoza Aroni, ndipo uiweyule kuti ikhale chopereka choweyula pamaso pa Chauta. Imeneyi ndiyo idzakhala gawo lako. Pambuyo pake upatule zigawo za nkhosa yopereka pa mwambo wodzozera Aroni ndi ana ake, ndiye kuti nganga yoperekedwa ngati chopereka choweyula ija, ndiponso ntchafu yoperekedwa ngati chopereka choweyula ija. Pa zimene Aisraele azipereka, zimenezi zikhale za Aroni ndi ana ake nthaŵi zonse. Alandire ndiwo ansembe zonsezi zochokera pa zopereka zamtendere za Aisraele pakuti ndizo mphatso zao za Aisraele kwa Chauta. “Zovala za Aroni zaunsembe zidzakhale za ana ake aamuna iyeyo atafa, kuti anawo azivala zimenezo pamene akudzozedwa ndi kulandira udindo wao. Mwana wa Aroni womloŵera m'malo kuti akhale wansembe, azidzavala zimenezi masiku asanu ndi aŵiri, pamene akuloŵa m'chihema chamsonkhano kukatumikira m'malo oyera. “Tsono utenge nkhosa yamphongo yophera mwambo woloŵera unsembe, uiphike m'malo oyera. Ndipo Aroni ndi ana akewo adye nyama ya nkhosa yamphongoyo, pamodzi ndi buledi wam'lichero uja pakhomo pa chihema chamsonkhano. Adzadye zonse zimene adazipereka kwa Chauta pa mwambo wopepesera machimo poŵadzoza ndi kuŵapatula. Munthu wamba asadyeko, chifukwa nzoyera. Nyama ikatsalako, kapena buledi akatsalako mpaka m'maŵa, utenthe. Asadye zimenezo chifukwa nzoyera. “Zonse zimene ndakulamulazi umchitire Aroni ndi ana ake aamuna omwe. Udzachite mwambo wakuŵapatula pa masiku asanu ndi aŵiri. Tsiku ndi tsiku uzipereka ng'ombe yamphongo yopepesera machimo, kuti machimowo akhululukidwe. Uyeretse guwalo pakuliperekera nsembe yopepesera machimo. Kenaka ulidzoze kuti likhale lopatulika. Pa masiku asanu ndi aŵiri uzipereka nsembe zoyeretsera guwalo, ndipo uzilipatula. Pambuyo pake guwalo lidzakhala loyera kwathunthu, ndipo chilichonse chimene chidzakhudze guwalo chidzaonongedwa chifukwa cha mphamvu ya kuyera kwake. “Pa guwa lansembe uziperekapo izi: nthaŵi zonse tsiku ndi tsiku, uzipereka anaankhosa aŵiri a chaka chimodzi. Mwanawankhosa wina uzimpereka m'maŵa, wina madzulo. Pamodzi ndi mwanawankhosa woyambayo, uzipereka kilogaramu limodzi la ufa wosalala watirigu wosakaniza ndi lita limodzi la mafuta abwino, ndiponso lita limodzi la vinyo ngati chopereka cha chakumwa. Tsono uzipereka mwanawankhosa wachiŵiriyo madzulo ndithu. Pamodzi ndi mwanawankhosayo, uziperekanso chopereka chachakudya ndi cha chakumwa, monga zam'maŵa zija, kuti zipereke fungo lokoma ndipo zikhale nsembe yopsereza yopereka kwa Chauta. Zopereka zopsereza zimenezi ziziperekedwa nthaŵi zonse pa mibadwo yonse. Muzizipereka pamaso pa Ine Chauta pa chipata choloŵera m'chihema chamsonkhano, kumene ndizidzakumana ndi anthu anga ndi kulankhula nawo. Kumeneko ndiko ndizidzakumana ndi Aisraele, ndipo malo amenewo azidzakhala oyeretsedwa chifukwa cha ulemerero wanga. Chihema chamsonkhanocho ndidzachisandutsa kuti chikhale chopatulika, pamodzi ndi guwa lomwe. Ndipo Aroni ndidzampatula pamodzi ndi ana ake aamuna, kuti akhale ansembe anga onditumikira. Ndidzakhala pakati pa anthu anga Aisraele, ndipo ndidzakhala Mulungu wao. Adzandidziŵa Ine Chauta amene ndidaŵatulutsa ku Ejipito kuti ndikhale pakati pao. Ine ndine Chauta, Mulungu wao. “Tsono upange guwa lofukizirapo lubani. Upange guwalo ndi matabwa a mtengo wa kasiya. Likhale lalibanda, kutalika kwake masentimita 46, muufupi mwake likhalenso masentimita 46, ndipo msinkhu wake ukhale wa masentimita 91. Nyanga zake zipangidwire kumodzi ndi guwalo. Ulikute ndi golide pamwamba pake, pa mbali zake zonse zinai ndi pa nyanga zakezo. Ndipo kuzungulira guwa lonselo ulembe mkombero wagolide. Upange mphete ziŵiri zagolide zonyamulira guwalo, ndipo uzilumikize ku guwa m'munsi mwa mkombero pa mbali ziŵiri, kuti mphiko zipisidwe m'mphetezo. Mphiko zimenezi ikhale ya mtengo wa kasiya, ndipo uikute ndi golide. Guwalo ulikhazike patsogolo pa nsalu yochinga bokosi lachipangano, patsogolo pa chivundikiro chimene chili pamwamba pa bokosi lachipangano. Pa malo ameneŵa ndi pamene ndizidzakumana nawe. M'maŵa mulimonse Aroni azifukiza lubani wa fungo lokoma, ndipo nthaŵi yomweyo azikonza nyale zija. Tsono pamene ayatsa nyalezo madzulo, azifukizanso lubani. Choncho pakhale kufukiza kosalekeza pamaso pa Chauta m'mibadwo yanu yonse. Paguwapo usafukizepo lubani wosaloledwa, kapena zopereka za nyama yopsereza kapena za zakudya. Usadzaperekenso pamenepo chopereka cha chakumwa. Aroni azidzachita mwambo wopepesera machimo pa nyanga za guwalo kamodzi pa chaka. Ndi magazi a nyama zija za nsembe zopepesera machimo azidzayeretsera guwa limeneli kamodzi pa chaka. Zimenezi zizidzachitikanso m'mibadwo yanu yonse. Guwa limeneli lidzakhala loyera kwambiri, lopatulikira Chauta.” Chauta adapitiriza kuuza Mose kuti, “Ukamachita kalembera wa ana aamuna a Aisraele, munthu aliyense adzapereke kwa Chauta choombolera moyo wake, kuti mliri uliwonse usadzamugwere pamene kalemberayo akuchitika. Aliyense woyenera kulembedwa m'kalemberamo adzapereke theka la sekeli, ndiye kuti ndalama zolemera ngati magaramu asanu ndi limodzi, kutsata muyeso wa ku Nyumba ya Mulungu (paja sekeli imodzi ikulingana ndi magera makumi aŵiri). Ndalama zimenezi zidzakhala zopereka kwa Chauta. Aliyense wolembedwa m'kalemberamo, wa zaka makumi aŵiri kapena kupitirira, adzapereke zimenezi kwa Chauta. Wolemera asadzapereke kopitirira, ndipo wosauka asadzapereke mochepera pa theka la sekeli, pamene muzikapereka kwa Chauta zopereka zimenezi, kuti muwombole moyo wanu. Ndalama zoombolerazo zochokera kwa Aisraele, mudzagwiritse ntchito ya m'chihema chamsonkhano. Zidzakumbutsa Chauta za Aisraele, ndipo zidzakhala zoombolera moyo wanu.” Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Upange beseni lamkuŵa losambira, ndipo phaka lake likhale lamkuŵa. Ulikhazike pakati pa chihema chamsonkhano ndi guwa, ndipo uthiremo madzi. Aroni ndi ana ake azisamba m'manja ndi kutsuka mapazi ao ndi madzi amenewo. Akamaloŵa m'chihema chamsonkhano, kapena kuyandikira guwalo pa ntchito yao yautumiki, ndi kumapereka kwa Chauta chopereka chopsereza, sadzafa malinga akasamba ndi madzi amenewo. Azisamba m'manja ndi kutsuka mapazi, kuti angafe. Limeneli ndi lamulo ndithu limene iwowo ndi adzukulu ao akutsogolo ayenera kumadzalitsata mpaka muyaya.” Chauta adauzanso Mose kuti, “Utenge zonunkhira bwino kwambiri zokwanira makilogaramu asanu ndi limodzi a mure wamadzi, makilogaramu atatu a zonunkhira bwino za mtundu wa kinamoni, makilogaramu atatu a nzimbe zonunkhira bwino, makilogaramu asanu ndi limodzi a kasiya (zonsezo potsata miyeso ya ku Nyumba ya Mulungu). Ndipo muwonjeze mafuta okwanira malita anai a olivi. Tsono zonsezi udzapangire mafuta odzozera. Udzaziphatikize pamodzi monga momwe amachitira munthu wopanga zonunkhira. Mafuta amenewo adzakhale mafuta oyera, odzozera. Udzadzoze chihema chamsonkhanocho ndi mafuta amenewo. Udzadzozenso bokosi lachipangano, tebulo ndi zipangizo zake zonse, choikaponyale pamodzi ndi zida zake, guwa lofukizirapo lubani, guwa lopserezapo zopereka, pamodzi ndi zipangizo zake, ndiponso beseni losambiramo lija ndi phaka lake lomwe. Zonsezi udzazipatula mwa njira imeneyi, ndipo zidzakhala zoyera kopambana. Ndipo chilichonse chokhudza zimenezi chidzaonongedwa chifukwa cha mphamvu ya kuyera kwake. Kenaka udzamdzoze Aroni pamodzi ndi ana ake, ndi kuŵapatula kuti akhale ansembe onditumikira. Tsono Aisraele onse udzaŵauze kuti, ‘Ameneŵa ndiwo adzakhale mafuta anga oyera odzozera pa mibadwo yanu yonse. Musadzadzozere anthu wamba, ndipo musadzapangenso mafuta ena ofanafana nawo. Ameneŵa ngoyera ndipo kwa inu adzakhalabe oyera ndithu. Munthu aliyense amene adzapange mafuta ena ofanafana nawo, kapena kudzozera munthu aliyense amene sali wansembe, adzamchotsa pakati pa anthu anzake.’ ” Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Utenge miyeso yofanafana ya zonunkhira bwino izi: sitakate, onika, galibanumu, ndi lubani weniweni. Uphatikize pamodzi zonsezi, ndipo upange lubani monga amachitira mmisiri wopanga zonunkhira. Athiremo mchere, ndipo akhale woyera ndi wopatulika. Upere gawo lina mosalala kwambiri, ndipo utatapako pang'ono, uike patsogolo pa bokosi lachipangano m'chihema chamsonkhano chokumanirako ndi anthu anga. Lubani ameneyu kwa inu akhale woyera kopambana. Ndipo lubani amene upangeyo potsata mapangidwe ake, asadzakhalire inuyo ai, koma adzakhale woyera wokhalira Chauta yekha. Ngati munthu wina apanga lubani wofanafana ndi ameneyu kuti amve fungo lake lokoma, azichotsedwa pakati pa anthu anzake.” Pambuyo pake Chauta adapitirira kuuza Mose kuti, “Ndasankha Bezalele mwana wa Uri, mdzukulu wa Huri, wa fuko la Yuda. Iyeyu ndampatsa mzimu wanga, kotero kuti ali ndi luso ndi nzeru, ndipo akudziŵa bwino ntchito zonse zaluso monga izi: kulemba mapulani a ntchito zaluso ndi kugwira ntchito ndi golide, siliva ndi mkuŵa. Akudziŵanso kuzokota miyala yogwira nayo ntchito, kujoba mitengo, ndi kuchita zaluso zonse. Ndasankhanso Aholiyabu mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani. Ndipo anthu ena onse aluso ndaŵapatsa nzeru zambiri zoti athe kupanga chinthu chilichonse chimene ndingakulamule kuti iwoŵa apange. Apange chihema chamsonkhano Ine ndi anthu anga, bokosi lachipangano, chivundikiro cha bokosi, pamodzi ndi zipangizo za chihema, tebulo ndi zipangizo zake, choikaponyale cha golide wabwino kwambiri, pamodzi ndi zipangizo zake, guwa lofukizirapo lubani, guwa la zopereka zopsereza, pamodzi ndi zipangizo zake, beseni losambira ndi phaka lake, zovala zopatulika za wansembe Aroni ndi za ana ake, zomavala pa nthaŵi imene akutumikira, mafuta odzozera ndiponso lubani wa fungo lokoma, zonsezo zokhalira malo oyera. Adzapange zinthu zonsezi monga ndakulamulira iwe.” Chauta adauzanso Mose kuti, “Uza Aisraele kuti, ‘Muzisunga Sabata, tsiku langa lopumula, chifukwa ndilo chizindikiro chamuyaya pakati pa Ine ndi inu ndi zidzukulu zanu, choonetsa kuti Ine ndine Chauta, amene ndimakuyeretsani. Motero muzisunga tsiku la Sabata, chifukwa ndi loyera kwa inu. Munthu aliyense wosalisunga, aphedwe. Aliyense wogwira ntchito pa tsiku limenelo adzachotsedwe pakati pa anthu anzake. Munthu agwire ntchito zake zonse pa masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi tsiku la Sabata lopumula, tsiku loyera la Chauta. Aliyense wogwira ntchito pa tsiku limeneli aphedwe. Aisraele azisunga tsiku la Sabatalo, ndipo mibadwo yonse yakutsogoloko izidzalisunga ngati pangano losatha. Chimenechi ndi chizindikiro chosatha pakati pa Ine ndi Aisraele, chakuti Ine Chauta ndidalenga kumwamba ndi dziko lapansi pa masiku asanu ndi limodzi, ndipo ndidapumula pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri.’ ” Chauta atatsiriza kulankhula ndi Mose pa phiri la Sinai lija, adampatsa Moseyo miyala iŵiri yaumboni, imene Mulungu mwini anali atalembapo kale. Anthu ataona kuti Mose wakhalitsako kuphiri osatsikako, adasonkhana kwa Aroni, ndipo adamuuza kuti, “Tiyeni mutipangire milungu yotitsogolera ife, chifukwa sitikudziŵa chomwe chamugwera Moseyo, amene adatitsogolera potitulutsa ku Ejipito kuja.” Tsono Aroni adauza anthuwo kuti, “Vulani nsapule zagolide kukhutu kwa akazi anu, kwa ana anu aamuna ndi ana anu aakazi omwe, ndipo mubwere nazo kwa ine.” Anthuwo adavuladi nsapule zao, ndipo adabwera nazo kwa Aroni. Tsono Aroni adalandira golideyo kumanja kwa anthuwo, ndipo adamsungunula, napanga fano la mwanawang'ombe m'chikombole. Ndipo anthu adayamba kufuula kuti, “Inu Aisraele, nayi milungu yanu imene idakutulutsani ku Ejipito.” Aroniyo ataona zimenezi, adapanga guwa patsogolo pa mwanawang'ombe wagolideyo. Tsono adalengeza kuti, “Maŵa padzakhala chikondwerero cholemekeza Chauta.” Choncho m'maŵa mwake, m'mamaŵa ndithu, adapereka nsembe zopsereza, nabweranso ndi nsembe zamtendere. Ndipo anthuwo adakhala pansi nayamba kudya ndi kumwa, kenaka adayambanso kuvina. Pamenepo Chauta adauza Mose kuti, “Fulumira, tsika phiri, chifukwa anthu ako amene udaŵatsogolera poŵatulutsa ku Ejipito aja, adziipitsa kwambiri. Asiya mwamsanga zonse zija zimene ndidaŵalamula kuti azichita. Adzipangira fano la mwanawang'ombe wa golide wosungunula, ndipo alipembedza ndi kuliphera nsembe, namanena kuti, ‘Inu Aisraele, nayi milungu yanu imene idakutulutsani ku Ejipito.’ ” Ndipo Chauta adaonjeza kuti, “Anthu ameneŵa ndikuŵadziŵa, ngokanika kwambiri. Nchifukwa chake tsono, undileke kuti ndiŵaononge chifukwa ndili wokwiya kwambiri, koma iweyo ndidzakusandutsa mtundu waukulu wa anthu.” Koma Mose adapepesa Chauta wake, nati, “Inu Chauta, chifukwa chiyani mukukwiyira anthu anu chotere, anthu amene mudaŵatulutsa mu ukapolo ku Ejipito kuja ndi mphamvu zanu zazikulu ndi dzanja lanu lamphamvu? Kodi mukufuna kuti Aejipitowo azidzanena kuti, ‘Adaŵatulutsa ku Ejipito ndi cholinga choipa choti akaŵaphere ku mapiri ndi kuŵaonongeratu pa dziko lapansi?’ Ukali wanu woyaka ngati motowo ubwezeni, ndipo musaŵaononge anthu anu. Kumbukirani atumiki anu aja Abrahamu, Isaki ndi Israele ndiponso zija mudaŵalonjezazi molumbira pa dzina lanu, pamene mudaŵauza kuti, ‘Ndidzakupatsani zidzukulu zambiri, zochuluka ngati nyenyezi zakuthambo. Zidzukulu zanuzo ndidzazipatsa dziko lonse limene ndidalonjeza. Dziko limeneli lidzakhala lao mpaka muyaya.’ ” Choncho Chauta adaleka chilango choopsa chimene adaati agwetsere anthu akewo. Mose adabwerera natsika phiri atanyamula miyala iŵiri ija yaumboni, yolembedwa mbali zonse ziŵiri. Imeneyi inali ntchito ya Mulungu, ndipo zolembedwazo adaalemba ndi Mulungu mwini mozizokota pamiyalapo. Tsono Yoswa adamva anthu akufuula, nauza Mose kuti, “Ndikumva phokoso lankhondo kumahemako.” Koma Mose adati, “Phokoso limenelo silikumveka ngati phokoso la opambana pa nkhondo, kapenanso kulira kwa ogonjetsedwa. Ndikumva phokoso la kuimba.” Mose atafika pafupi ndi mahema aja, ndi kuwona mwanawang'ombe uja ndi anthu ovina, adakalipa kwambiri. Adaponya pansi miyala inali m'manja mwake ija, naiphwanya patsinde pa phiri paja. Pomwepo adakatenga mwanawang'ombe amene Aroni adapanga, namperapera ngati ufa, ndipo adakamtaya m'madzi. Tsono Aisraele aja adaŵamwetsa madziwo. Kenaka Mose adafunsa Aroni uja kuti, “Kodi anthu ameneŵa adakuchita zotani iwe, kuti uŵachimwitse koopsa chotere?” Aroni adayankha kuti, “Musakwiyire ine mbuyanga. Mumaŵadziŵa anthu ameneŵa kuti ngovuta. Iwoŵa adandiwuza kuti, ‘Tipangireni milungu yoti ititsogolere ife, chifukwa sitikudziŵa chomwe chamgwera Mose, amene adatitsogolera potitulutsa ku Ejipito.’ Tsono ine ndidaŵauza kuti, ‘Aliyense amene ali ndi golide abwere naye.’ Ndipo amene anali nazo zinthu zopangidwa ndi golide adandipatsa. Ndidaziponya pa moto, ndipo ndidapanga fano la mwanawang'ombe lija.” Mose adaonadi kuti anthuwo ngosokonezeka, (chifukwa Aroni adaaŵalekerera, mpaka iwo kusanduka anthu oŵanyodola pakati pa adani ao). Moseyo adaimirira pa chipata cha mahema aja ndipo adafuula mokweza nafunsa kuti, “Kodi ndani akufuna Chauta? Bwerani kuno.” Pompo Alevi onse adadzasonkhana kwa iye, ndipo Mose adaŵauza kuti, “Chauta, Mulungu wa Aisraele, akunena kuti, ‘Aliyense mwa inu atenge lupanga, ndipo mupite ku mahema ndi kuloŵa m'zipata zonse. Aliyense mwa inu akaphe mbale wake kapena bwenzi lake kapena mnansi.’ ” Aleviwo adachitadi monga momwe Mose adaŵalamulira, ndipo amuna 3,000 adaphedwa pa tsiku limenelo. Apo Mose adauza Aleviwo kuti, “Lero lino mwadzipatula nokha kuti mukhale ansembe otumikira Chauta, pakupha ana anu ndi abale anu omwe. Motero Chauta akudalitsani lero.” M'maŵa mwake Mose adauza anthu kuti, “Inu mudachimwa koopsa. Koma tsopano ndidzapita kwa Chauta ku phiri, ndipo nditakupemphererani, kapena angathe kukukhululukirani machimo anu.” Tsono Mose adabwerera kwa Chauta nakanena kuti, “Anthu aŵa adachimwa koopsa. Adadzipangira milungu yagolide. Koma tsopano, chonde muŵakhululukire machimo ao. Mukapanda kuŵakhululukira, chonde mufafanize dzina langa m'buku m'mene mudalemba.” Apo Chauta adauza Mose kuti, “Yekhayo amene wandilakwira Ine, ndiye amene ndidzachotse dzina lake m'buku langa. Tsopano pita uŵatsogolere anthuwo ku malo amene ndidakuuza. Kumbukira kuti mngelo wanga adzakutsogolera, koma tsiku likubwera limene ndidzaŵalange iwowo chifukwa cha machimo ao.” Motero Chauta adatumiza nthenda pa anthuwo, chifukwa choti adakakamiza Aroni kuti aŵapangire fano la mwanawang'ombe. Pambuyo pake Chauta adauza Mose kuti, “Uchokeko kuno pamodzi ndi anthu amene udabwera nawo kuchokera ku Ejipito, ndipo upite ku dziko limene ndidalonjeza kuti ndidzapatsa Abrahamu, Isaki ndi Yakobe. Pa nthaŵi imeneyo ndidaŵauza iwowo kuti, ‘Dziko limeneli ndidzalipatsa kwa zidzukulu zanu.’ Ndidzatuma mngelo patsogolo pako, ndipo ndidzapirikitsa Akanani, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi. Pitani ku dziko lamwanaalirenji. Koma Ine sindidzapita nanu chifukwa ndinu anthu okanika, ndipo ndingathe kukuwonongani panjira.” Tsono anthu atamva mau oopsaŵa, adayamba kulira, ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe amene adavala zovala zokongola. Ndiye kuti Chauta anali atauza Mose kuti, “Uza Aisraelewo kuti, ‘Ndinu anthu okanika. Ndikadapita nanu pamodzi, ngakhale kamphindi kakang'ono kokha, bwenzi nditakuwonongani kwathunthu. Tsopano vulani zokongoletsa zanu, ndipo ndidzadziŵa choti ndingathe kukuchitani.’ ” Motero kuyambira ku phiri lija la Horebu, Aisraele sadavalenso zokongoletsa. Mose ankatenga chihema chija ndi kukachimanga kunja kwake kwa mahema, chapatali ndithu. Tsono adachitcha chihemacho dzina loti, “Chihema chamsonkhano.” Aliyense wofuna kukafunsa kanthu kwa Chauta ankatuluka kumahemako, napita ku chihema chamsonkhanocho. Nthaŵi zonse Mose akamapita kuchihemako, anthu onse ankaimirira. Tsono aliyense ankangoimirira pakhomo pa hema lake, namayang'ana Moseyo mpaka ataloŵa m'chihema chokumaniranako ndi Chauta chija. Mose ataloŵa m'chihema muja, mtambo unkatsika nuphimba pakhomo pa chihemacho, ndipo Chauta ankalankhula ndi Mose kuchokera mumtambomo. Ndipo anthu ankati akaona mtambowo pa khomo la chihemacho, ankaimirira ndi kupembedza, aliyense pa khomo la hema lake. Choncho Chauta ankalankhula ndi Mose pamasompamaso, monga momwe munthu amalankhulira ndi bwenzi lake. Tsono pambuyo pake Mose ankabwerera kumahema komweko. Koma mnyamata wina, dzina lake Yoswa, mwana wa Nuni, amene anali mtumiki wa Mose, sankachoka kuchihemako. Mose adauza Chauta kuti, “Mwakhala mukundiwuza kuti ndiŵatsogolere anthuŵa ku dzikolo, koma simudandiwuze amene mudzamtuma kuti apite nane. Komabe mwanena kale kuti, ‘Ndikukudziŵa bwino iwe, ndipo ndakondwa nawe.’ Nchifukwa chake tsono ndikukupemphani kuti ngati mwandikomera mtima, mundilangize njira zanu kuti ndikudziŵeni ndipo mupitirize kundikomera mtima. Kumbukiraninso kuti mtundu wa anthu uwu ndi wanu ndithu.” Ndipo Mulungu adati, “Ine ndemwe ndidzapita nawe pamodzi, ndipo ndidzakupatsa mtendere.” Apo Mose adauza Chauta kuti, “Mukapanda kupita nafe limodzi, musatilole kuti tichoke pano. Nanga zidzadziŵika bwanji kuti mwandikomera mtima ine pamodzi ndi anthu anu? Kodi si chifukwa chakuti mumapita nafe, ine pamodzi ndi anthu anu, kuti tizikhala osiyana ndi anthu ena onse a pa dziko lapansi?” Tsono Chauta adauza Moseyo kuti, “Ndidzachita monga wanena, chifukwa ndakukomera mtima, ndipo ndikukudziŵa bwino.” Apo Mose adapempha Chauta kuti, “Chonde mundiwonetse ulemerero wanu.” Pamenepo Chauta adayankha kuti, “Ndikudzakuwonetsa ulemerero wanga wonse, ndipo ndidzatchula dzina langa loti Chauta pamaso pako. Ndidzakomera mtima amene nditi ndimkomere mtima, ndipo ndidzachitira chifundo amene nditi ndimchitire chifundo.” Chauta adaonjeza kuti, “Koma sungathe kuwona nkhope yanga, chifukwa palibe munthu angathe kundiwona Ine, nakhala moyo.” Adapitirira kunenanso kuti, “Pafupi ndi Ine pano pali thanthwe, iwe uimirire pathanthwepo. Tsono ulemerero wanga ukamapita, ndikuika mu mng'alu wa thanthwe, ndipo ndikuphimba ndi dzanja langa mpaka nditabzola. Kenaka ndichotsa dzanja langa, ndipo undiwona kumsana, koma nkhope yanga suiwona ai.” Chauta adauzanso Mose kuti, “Sema ina miyala ngati iŵiri yakale ija, kuti ndilembepo mau omwe anali pa miyala yoyamba udaphwanya ija. Ukonzeke m'mamaŵa, ndipo nthaŵi yam'maŵa, ukwere phiri la Sinai kuti udzakumane nane pamwamba pa phiripo. Usabwere ndi wina aliyense, ndipo wina asaoneke pa mbali iliyonse ya phirilo. Nkhosa kapena ng'ombe zisadzadye pa tsinde la phirilo.” Motero Mose adasema ina miyala iŵiri ngati yakale ija, ndipo kutacha m'maŵa, adakwera phiri la Sinai monga momwe Chauta adamlamulira. Anali atanyamula miyala iŵiri ija. Tsono Chauta adatsika mu mtambo, naimirira pomwe panali iyepo, ndipo adatchula dzina lake loti Chauta. Adayenda pamaso pa Mose nanena mokweza kuti, “Chauta, Chauta, Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika, ndiponso wokhulupirika kwa anthu ake. Amaonetsa chikondi chake kwa anthu zikwi zambirimbiri, ndipo amaŵakhululukira mphulupulu zao, zoipa zao, ndi machimo ao. Koma sadzalekerera ochimwa, ndipo adzalanga ana ndi zidzukulu chifukwa cha zoipa za atate ao, mpaka mbadwo wachitatu ndi wachinai.” Pamenepo Mose adagwada pansi napembedza. Kenaka adati, “Ngati mwandikomera mtima, Inu Chauta, ndikukupemphani kuti mupite nafe. Anthuŵa ngokanika, koma Inu mutikhululukire zolakwa zathu ndi machimo athu, ndipo mutilandire ife, kuti tikhale anthu anu.” Pambuyo pake Chauta adati, “Ndidzachita nanu chipangano. Ndidzachita zozizwitsa zazikulu pamaso pa anthu ako onseŵa, zimene sizidachitikepo ndi kale lonse pa dziko lonse lapansi, pakati pa mitundu ina yonse. Anthu onse amene ali ndi iweŵa adzaona zimene Ine Chauta ndingathe kuchita, chifukwa zimene ndidzachita kudzera mwa iwe nzoopsa zedi. “Muzimvera malamulo amene ndakulamulani leroŵa. Ndidzapirikitsa Aamori, Akanani, Ahiti, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi. Musamale kuti musachite chipangano ndi anthu a ku dziko limene mukupitakolo, kuwopa kuti chingadzakhale msampha wokuchimwitsani. Muzigwetsa maguwa ao, muwononge miyala yao yopatulika imene adaimiritsa, ndipo mugwetse mitengo yao yopatulika yopembedzerapo. Musadzapembedze mulungu wina aliyense, chifukwa Chauta amene dzina lake ndi Kansanje, ndi Mulungu wansanjedi. Anthu a ku dziko limenelo, musadzachite nawo chipangano, chifukwa akamadziipitsa popembedza milungu yao nkumaiphera nsembe, kapena adzakuitanani kuti mudye nao chakudya cha nsembe zaozo. Mwina ana anu aamuna angathenso kumadzakwatira ana ao aakazi. Tsono akazi ameneŵa akamadziipitsa potumikira milungu yao, adzakopa ana anu aamuna kuti azidzatumikiranso milungu yaoyo. “Musadzipangire milungu yosungunula. “Muzichita chikondwerero cha buledi wosafufumitsa monga ndidakulamulirani. Muzidzadya buledi wosafufumitsa pa masiku asanu ndi aŵiri pa mwezi wa Abibu, chifukwa ndi mwezi umenewu pamene inu mudachokako ku Ejipito kuja. Mwana wamphongo aliyense woyamba kubadwa ndi wanga, pamodzi ndi wa zoŵeta yemwe, ndiye kuti ng'ombe ndi nkhosa zanu zomwe. Koma muzidzaombola mwana woyamba kubadwa wa bulu, pakupereka nkhosa m'malo mwake. Mukapanda kumuwombola, muzidzamthyola khosi. Mwana aliyense wachisamba wamwamuna, muzidzachita choombola. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaonekere pamaso panga opanda kanthu kumanja kodzapereka. “Muzigwira ntchito pa masiku asanu ndi limodzi, koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, musagwire ntchito iliyonse, ngakhale pa nthaŵi yolima kapena yokolola. Muzichita chikondwerero cha masabata, ndi chikondwerero cha kukolola tirigu woyambirira, ndi chikondwerero cha kututa zokolola zonse pakutha pake pa chaka. Amuna onse azibwera pamaso pa Ine Chauta, Mulungu wa Aisraele, katatu pa chaka. Ndidzapirikitsa mitundu inayo pamene inu mukufika, ndi kukuziriza malire a dziko lanu. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzafune kulanda dziko lanulo nthaŵi zitatuzo za pa chaka, pamene mudzadziwonetse pamaso pa Ine Chauta, Mulungu wanu. “Musapereke buledi wofufumitsa pamene mukupereka kwa Ine magazi a nsembe yanga. Nyama iliyonse yophera nsembe ya Paska, musaisunge mpaka m'maŵa. Muzibwera ndi zokolola zoyamba ndi zabwino kwambiri ku Nyumba ya Chauta, Mulungu wanu. Musaphike kamwanakanyama mu mkaka wa make.” Chauta adauzanso Mose kuti, “Lemba mauŵa, chifukwa potsata mau ameneŵa, ndikuchita chipangano ndi iwe ndi Aisraele onse.” Tsono Mose adakhala pamodzi ndi Chauta kumeneko masiku makumi anai, usana ndi usiku, osadya kanthu. Ndipo Chautayo adalemba pa miyala iŵiri ija mau onse a chipanganocho, ndiye kuti Malamulo Khumi aja. Pamene Mose adatsika phiri la Sinai atanyamula miyala iŵiri yaumboni ija, sadadziŵe kuti nkhope yake njoŵala chifukwa cholankhula ndi Chauta. Aroni ndi anthu onse aja atayang'ana Mose, adaona kuti nkhope yake njoŵala. Ndipo adachita mantha osafuna kumuyandikira. Koma Mose adaŵaitana, ndipo Aroni pamodzi ndi atsogoleri a Aisraele aja atabwera kwa iye, Moseyo adayamba kulankhula nawo. Pambuyo pake Aisraele onse adasendera pafupi, ndipo Mose adaŵapatsa malamulo onse amene Chauta adaamuuza ku phiri la Sinai lija. Mose atamaliza kulankhula nawo, adadziphimba kumaso. Nthaŵi zonse Moseyo ankati akaloŵa m'chihema kukalankhula ndi Chauta, ankachotsa nsalu yophimba kumaso ija mpaka atatuluka. Tsono atatuluka, ankauza Aisraele aja zonse zimene Chauta wamulamula kuti anene. Ndipo anthuwo ankaona kuti nkhope yake njoŵala, koma Moseyo ankadziphimbanso kumaso mpaka nthaŵi ina yakuti apitenso kukalankhula ndi Chauta. Mose adaitana Aisraele onse naŵauza kuti, “Chauta akukulamulani kuti, Muzigwira ntchito zanu pa masiku asanu ndi limodzi. Koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri, lidzakhala la Sabata, tsiku lanu lopumula, loperekedwa kwa Chauta. Munthu aliyense wogwira ntchito pa tsiku limenelo, adzaphedwa. Pa tsiku la Sabata limenelo, musamasonkha ndi moto womwe m'nyumba mwanu.” Mose adauza Aisraele onse aja kuti, “Chauta akukulamulani kuti, ‘Muzipereka zopereka kwa Chauta. Tsono aliyense amene ali ndi mtima wofuna kupereka, azibwera ndi zopereka izi: golide, siliva, mkuŵa, thonje lobiriŵira, lofiirira ndi lofiira. Azibweranso ndi nsalu yokoma yabafuta, nsalu zopangidwa ndi ubweya wambuzi, chikopa chankhosa chonyika mu utoto wofiira, zikopa zambuzi, matabwa a mtengo wa kasiya, mafuta anyale, zonunkhira zopangira mafuta odzozera, ndiponso zopangira lubani wonunkhira bwino, miyala ya mtundu wa onikisi ndi ina yokoma yoika pa chovala chaunsembe cha efodi ndiponso pa chovala chapachifuwa.’ ” “Anthu onse aluso pakati panupa abwere, ndipo apange zonse zimene Chauta adalamula. Apange chihema cha Chauta, hema lake pamodzi ndi chophimbira chake, ngoŵe zake zokoŵera, mafulemu ake, mitanda yake, nsanamira zake pamodzi ndi masinde ake omwe. Apangenso bokosi lachipangano ndi mphiko zake, chivundikiro chake cha bokosilo ndi nsalu zotchinga bokosilo; tebulo, pamodzi ndi mphiko zake ndi zipangizo zake, ndiponso buledi woperekedwa kosalekeza kwa Mulungu; choikaponyale ndi zipangizo zake, nyale zake ndi mafuta a nyalezo; guwa lofukizirapo lubani ndi mphiko zake, mafuta odzozera, lubani wa fungo lonunkhira bwino, ndiponso nsalu zochingira za pa chipata cha chihema cha Chauta. Apangenso guwa la zopereka zopsereza pamodzi ndi chitsolo cha sefa yamkuŵa, mphiko zake ndi zipangizo zake zomwe, beseni losambira ndi phaka lake lomwe; nsalu zochinga bwalo, nsanamira pamodzi ndi masinde ake omwe, nsalu za pa chipata choloŵera ku bwalo, zikhomo zake pamodzi ndi zingwe za chihema cha Chauta ndi za bwalo lake; nsalu zokoma kwambiri zovala anthu otumikira m'malo opatulika, ndiponso zovala zopatulika za wansembe Aroni ndi za ana ake, akamatumikira ngati ansembe.” Tsono Aisraele onse aja adachoka ndi kumsiya Mose. Ndipo munthu aliyense, monga momwe mtima wake unkafunira, adabwera kwa Chauta ndi zopereka zopangira chihema chamsonkhano cha Chauta. Adabwera nazo zonse zogwiritsira ntchito potumikira, ndi zonse zopangira zovala zopatulika. Kudabwera amuna ndi akazi omwe. Munthu aliyense malinga ndi kufuna kwake adabwera ndi zokometsera zomangira zovala, nsapule zakukhutu, mphete, ukufu wam'khosi, ndi zokometsera zina zagolide. Munthu aliyense adabwera ndi zagolide zimene adazipatula kuti zikhale zopereka zoweyula pamaso pa Chauta. Munthu aliyense amene anali ndi nsalu zobiriŵira, zofiirira ndi zofiira, bafuta wa thonje losalala kwambiri, nsalu za ubweya wambuzi, zikopa zankhosa zonyika mu utoto wofiira, ndi zikopa zambuzi, adabwera nazo kwa Chauta. Aliyense adabwera ndi zimene anali nazo. Anthu onse amene anali ndi siliva kapena mkuŵa, zonsezo adabwera nazo kwa Chauta. Onse amene anali ndi matabwa a mtengo wa kasiya wogwiritsira ntchito pomangapo, adabwera nawo ndithu. Akazi onse aluso adaomba nsalu za thonje lobiriŵira, lofiirira ndi lofiira. Adabweranso ndi bafuta wa thonje losalala kwambiri. Akazi onse alusowo adaombanso nsalu za ubweya wambuzi. Ndipo atsogoleri adabwera ndi miyala ya onikisi ndi miyala ina yoika pa chovala cha efodi ndiponso pa chovala chapachifuwa. Adaperekanso zonunkhira, mafuta anyale, mafuta odzozera ndiponso lubani wa fungo lokoma. Motero Aisraele onse, amuna ndi akazi omwe, amene adafuna ndi mtima wao wonse kupereka zao ku ntchito zimene Chauta adalamula kudzera mwa Mose, adabwera ndi zopereka zao kwa Chauta. Pambuyo pake Mose adauza Aisraele kuti, “Chauta wasankhula Bezalele, mwana wa Uri, mdzukulu wa Huri, wa fuko la Yuda. Chauta wadzaza Bezaleleyo ndi mzimu wa Mulungu, kotero kuti ali ndi luso ndi nzeru, ndiponso ndi wodziŵa ntchito zonse zaluso. Amadziŵanso kulemba mapulani a ntchito zaluso ndi kugwira ntchito ndi golide, siliva ndi mkuŵa. Amadziŵa kusema miyala yakongoletsera, kujoba matabwa, ndi kuchita ntchito zonse zaluso. Tsono Chauta wapatsa nzeru kwa iyeyo ndi kwa Oholiyabu mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani, kuti aziphunzitsa ena luso laolo. Iwoŵa adapatsidwa luso lalikulu, kuti achite ntchito za mitundu yonse zimene amachita anthu ozokota, amisiri a ntchito zaluso, anthu oomba nsalu za bafuta wa thonje losalala kwambiri. Akudziŵadi kugwira ntchito zonse, ndipo angathenso kuganizira ntchito zonse zaluso. “Ndipo Bezalele, Oholiyabu, pamodzi ndi aluso onse amene Chauta adaŵapatsa luso ndi nzeru zodziŵira kupanga zofunika zonse zomangira malo opatulika, adzapanga zonse iwowo, monga momwe Chauta adalamulira.” Pamenepo Mose adaitana Bezalele, Oholiyabu ndi onse aluso amene Chauta adaŵapatsa nzeru, ndiponso onse amene anali okonzeka kuthandiza. Ndipo Mose adaŵapatsa zopereka zonse zaufulu zomangira malo opatulika zimene Aisraele adabwera nazo. Koma Aisraelewo ankapatsabe Mose zopereka zao m'maŵa mulimonse. Tsono aluso onse amene ankagwira ntchito zomanga malo opatulika aja, aliyense potsata luso lake, adasiya ntchito zao, nadzauza Mose kuti, “Anthu akubwera ndi zipangizo za ntchitoyi zochuluka, kuposa m'mene zidzafunikire pogwira ntchito imene Chauta adalamula kuti ichitike.” Motero Mose adalamula anthu m'mahema monse kuti, “Mwamuna aliyense ndi mkazi aliyense asaperekenso zopereka zomangira malo opatulika.” Motero anthu adaleka kubwera ndi zopereka. Zimene anali atazisonkhanitsa zidachuluka kuposa zimene zinkafunika kuti amalize ntchitoyo. Tsono amuna onse aluso pakati pa anthu ogwira ntchitoyo, adapanga chihema cha Chauta ndi nsalu khumi za bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, ndiponso ndi nsalu zobiriŵira, zofiirira ndi zofiira. Pa nsalu zonsezo adapetapo zithunzi za akerubi. M'litali mwa nsalu iliyonse munali mamita 13, ndipo muufupi mwake munali masentimita 183. Zonsezo zinali zofanana. Ndipo adasokerera nsalu zisanu, kuti zikhale chinsalu chimodzi, zisanu zinazonso adazisokerera nkukhalanso chinsalu chimodzi. Pambuyo pake adasoka magonga a tinsalu tobiriŵira m'mphepete mwa chimodzi kubwalo kwake, ndipo adachitanso chimodzimodzi ndi chinacho. Adasoka magonga makumi asanu pa chinsalu choyambacho, ndi magonga ena makumi asanu pa chinsalu chinacho, mopenyana ndi magonga a chinsalu choyamba aja. Kenaka adapanga ngoŵe zokoŵera zagolide makumi asanu, nalumikiza nsalu zazikulu ziŵirizo ndi ngoŵezo. Pamenepo chihema cha Chauta chidakhala chimodzi. Pambuyo pake adasoka nsalu khumi ndi imodzi za ubweya wambuzi, napanga chophimbira pamwamba pa chihemacho. M'litali mwa nsalu iliyonse munali mamita 14, ndipo muufupi mwake munali masentimita 183. Zonsezo zinali zofanana. Tsono adasokerera nsalu zisanu nkukhala chinsalu chimodzi, ndipo nsalu zinazo zisanu ndi imodzi, adazisokereranso kuti zikhale chinsalu chimodzi. Adasokanso magonga makumi asanu m'mphepete mwake mwa nsalu yomalizira ya chinsalu choyambacho, ndi magonga ena makumi asanu m'mphepete mwa chinsalu chinacho. Kenaka adapanga ngoŵe zokoŵera zokwanira makumi asanu zamkuŵa zolumikizira pamodzi nsalu ziŵirizo, kuti apange chinsalu chimodzi chophimbira chihema. Ndipo adapanga chophimbira china chofiira cha zikopa za nkhosa zamphongo. Potsiriza adapanganso chophimbira china cha zikopa zofeŵa, nkuchiika pamwamba pa zophimba zina zonse. Pambuyo pake adapanga mafulemu a chihemacho ndi matabwa a mtengo wa kasiya. M'litali mwa fulemu lililonse munali mamita anai ndi theka, ndipo muufupi mwake munali masentimita 69. Thabwa lililonse linali ndi zolumikizira ziŵiri, ndipo mafulemu onse adaŵapanga ndi zolumikizira ziŵiri. Mafulemu onse adaŵapanga ndi zolumikizira zotere. Pa mbali yakumwera adapanga mafulemu makumi aŵiri, ndi masinde makumi anai chapansi pake. Pa fulemu lililonse adapanga masinde aŵiri asiliva, ogwirana ndi zolumikizira ziŵiri zija. Pa mbali yakumpoto ya chihemacho adapanganso mafulemu makumi aŵiri ndi masinde ake makumi anai asiliva, masinde aŵiri pansi pa fulemu lililonse. Adapanganso mafulemu asanu ndi limodzi kumbuyo kwake kwa chihemacho chakuzambwe, ndiponso mafulemu aŵiri am'ngodya, kumbuyo kwake kwa chihemacho. Mafulemu aŵiri am'ngodyawo anali olumikizika pansi pake ndi ogwirizana mpaka pamwamba ku ngoŵe yokoŵera yoyamba ija. Ndimo m'mene mafulemu aŵiri opanga ngodya ziŵiri aja adapangidwira. Motero panali mafulemu asanu ndi atatu, ndi masinde asiliva 16, aŵiri pansi pa fulemu lililonse. Kenaka adapanga mitanda ya matabwa a mtengo wa kasiya, isanu ya mafulemu a mbali imodzi ya chihema, isanu ya mafulemu a mbali inayo, ndiponso isanu ya mafulemu a mbali yakuzambwe, kumbuyo kwake kwa chihema. Tsono adapanga mtanda wapakati chapakatimpakati, wogwira mafulemuwo kuyambira ku mbali imodzi ya chihema mpaka mbali ina. Mafulemu onsewo adaŵakuta ndi golide, ndipo adamangapo mphete zagolide zopisiramo mitanda ija, imene adaikutanso ndi golide. Pambuyo pake adapanga nsalu yochingira yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso nsalu ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, ndipo adapetapo zithunzi za akerubi. Adapanga nsanamira zinai zakasiya zogwirizira nsalu yochingira ija. Nsanamirazo zinali zitakutidwa ndi golide, ndipo adaika ngoŵe zokoŵera ku nsanamirazo. Adapanga masinde anai asiliva ogwirizira nsanamirazo. Pa chipata choloŵera m'chihemamo, adaikapo nsalu yochinga yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso nsalu ya bafuta wosalala, wopikidwa bwino ndi wopetedwa mwaluso. Tsono adapanga nsanamira zisanu zokhala ndi ngoŵe zokoŵera nsaluyo, ndipo mitu yake ndi mitanda yake adaikuta ndi golide, koma masinde ake anali amkuŵa. Pambuyo pake Bezalele adapanga bokosi lachipangano ndi matabwa a mtengo wa kasiya. Kutalika kwake kunali masentimita 114, muufupi mwake masentimita 69, msinkhu wake masentimita 69. Tsono lonselo adalikuta ndi golide m'kati mwake ndi kunja komwe, ndipo adalemba mkombero wagolide kuzungulira bokosi lonselo. Adapanga mphete zinai zagolide zonyamulira, nazimangirira ku ngodya zinai za bokosilo, uku ziŵiri uku ziŵiri. Adapanga mphiko zinai za matabwa a mtengo wa kasiya, nazikuta ndi golide, ndipo mphikozo adazipisa m'mphete zija pa mbali zonse ziŵiri za bokosilo, kuti azinyamulira. Kenaka adapanga chivundikiro cha golide wabwino kwambiri, kutalika kwake masentimita 114, muufupi wake masentimita 69. Pa nsonga zake ziŵiri za chivundikirocho, adazokotapo akerubi aŵiri a golide wosula ndi nyundo, wina uku wina uku. Adaŵapangira kumodzi ndi chivundikirocho. Mapiko a akerubiwo adaŵatambalitsa pamwamba, kuphimba chivundikiro chija. Adakhala choyang'anana, ndipo aliyense anali kuyang'anananso ndi chivundikirocho. Bezalele adapanganso tebulo la matabwa a mtengo wa kasiya, m'litali mwake masentimita 91, muufupi mwake masentimita 46, ndipo mumsinkhu mwake masentimita 69, Tsono adalikuta ndi golide wabwino kwambiri, nalemba mkombelo wagolide kuzungulira tebulo lonselo. Adapanga fulemu lagolide pozungulira, muufupi mwake munali ngati kuyesa chikhatho, nalemba mkombero wagolide molizungulira. Kenaka adapanganso mphete zinai zagolide za tebulolo, naziika pa ngodya zinai ku miyendo ya tebulolo. Mphete zopisiramo mphiko ponyamula tebulolo, zinali pafupi ndi fulemu lija. Adapanga mphiko za matabwa a mtengo wa kasiya, nazikuta ndi golide. Adapanganso ziŵiya za golide wabwino kwambiri za pa tebulolo, monga mbale, zikho, mitsuko ndi mabeseni ogwiritsira ntchito pa zopereka zamadzi. Pambuyo pake adapanga choikaponyale cha golide wabwino kwambiri. Tsinde lake ndi thunthu lake zinali zagolide, ndipo zonse zinali zosula ndi nyundo. Zikho zake, ndiye kuti nkhunje ndi maluŵa ake, adazipangira kumodzi ndi choikaponyalecho. Pa mbali zake adapanga nthambi zisanu ndi imodzi, zitatu pa mbali iliyonse. Iliyonse mwa nthambizo inali ndi maluŵa atatu, opangidwa ngati maluŵa amtowo, okhala ndi nkhunje ndi maluŵa ake. Pa thunthu lake la choikaponyalecho panali zikho zinai zonga maluŵa amtowo okhala ndi nkhunje zake ndi maluŵa ake. Panali nkhunje imodzi pansi pa magulu atatu a nthambi zija, zitapatulidwa ziŵiriziŵiri. Nkhunjezo, pamodzi ndi nthambizo, zidapangidwira kumodzi ndi choikaponyale chija. Chonsecho chinali chinthu chimodzi chagolide, chosula ndi nyundo. Ndipo adapanga nyale zisanu ndi ziŵiri za pa choikaponyalecho, napanganso mbanira ndiponso zoolera phulusa za golide wabwino kwambiri. Popanga choikaponyalecho, pamodzi ndi zipangizo zake zonsezo, adagwiritsa ntchito makilogaramu 34 a golide wabwino kwambiri. Guwa lofukizirapo lubani adalipanga ndi matabwa a mtengo wa kasiya. Linali lalibanda, muutalika mwake munali masentimita 46, muufupi mwake masentimita 46, msinkhu wake masentimita 91, ndipo nyanga zake zidapangidwira kumodzi ndi guwalo. Adakuta guwa lonse ndi golide wabwino kwambiri pamwamba pake, pa mbali zake ndi pa nyanga zake zomwe. Kuzungulira guwa lonselo, adalemba mkombero wagolide. Adapanga mphete ziŵiri zagolide zonyamulira guwalo, ndipo adazilumikiza ku mbali zonse ziŵiri za guwa, pansi pa mkombero uja, kuti apisemo mphiko zonyamulira. Mphikozo adazipanga ndi matabwa a mtengo wa kasiya, naikuta ndi golide. Adapanganso mafuta oyera odzozera, ndiponso zofukizira za fungo lokoma. Mapangidwe ake adachita monga momwe ankachitira mmisiri wopanga zonunkhira. Pambuyo pake adapanga guwa la nsembe zopsereza la matabwa a mtengo wa kasiya. Linali lalibanda, muutali mwake munali masentimita 229, muufupi mwakenso ngati masentimita 229 mbali zonse zinali zofanana, msinkhu wake ngati masentimita 137. Pa ngodya zake zinai adapangapo nyanga zotuluka m'guwalo, mwakuti zidangolumikizika nkukhala chinthu chimodzi ndi guwalo. Ndipo guwa lonselo adalikuta ndi mkuŵa. Adapanganso zipangizo zonse za guwalo, mbale zolandirira phulusa, mafosholo, mabeseni, ngoŵe zokoŵera zinthu, ndiponso ziwaya zosonkhapo moto. Zonsezo zidapangidwa ndi mkuŵa. Tsono adapanga chitsulo cha sefa, cha guwa lansembelo, cholukidwa ndi mkuŵa wokhawokha, ndipo adachiika kunsi kwake kwa chibumi cha guwa, kuti chifike pakatimpakati pa guwalo. Adapanga mphete zinai ndipo adazilumikiza ku ngodya zinai za sefa ija, kuti apisemo mphiko zonyamulira. Adasema mphiko zonyamulira za mtengo wa kasiya, nazikuta ndi mkuŵa. Tsono guwalo pomalinyamula, mphikozo ankazilonga m'mphete zija, pa mbali zonse ziŵiri za guwa. Guwalo adalipanga ndi matabwa, ndipo adalijoba m'kati mwake. Ndipo adapanga beseni lamkuŵa losambira, pamodzi ndi phaka lake. Adapanga zimenezi ndi akalilole a akazi amene ankatumikira ku chipata choloŵera m'chihema chamsonkhano chija, kumene Chauta ankakumanako ndi anthu ake. Tsono adapanga bwalo. Nsalu zake zochingira bwalolo chakumwera kwake zinali za bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, ndipo kutalika kwake kunali mamita 46. Nsanamira zake makumi aŵiri, pamodzi ndi masinde ake makumi aŵiri, zonsezo zinali zamkuŵa, koma ngoŵe za pa nsanamirazo, pamodzi ndi mitanda yake, zinali zasiliva. Ku mbali yakumpoto kunali nsalu zochingira, kutalika kwake mamita 46. Nsanamira zake makumi aŵiri ndi masinde makumi aŵiri zinali zamkuŵa. Koma ngoŵe za pa nsanamirazo, pamodzi ndi mitanda yake, zinali zasiliva. Pa mbali yakuzambwe panali nsalu zochingira, kutalika kwake mamita 23, ndi nsanamira zake khumi ndi masinde khumi. Ngoŵe zake ndiponso mitanda yake zinali zasiliva. Pa mbali inayo yakuvuma panalinso mamita 23. Panali nsalu zochinga pa mbali imodzi ya chipata, zotalika mamita asanu ndi aŵiri, zokhala ndi nsanamira zake zitatu ndi masinde atatu. Pa mbali inayo panali chimodzimodzi. Choncho pa mbali zonse ziŵirizo za chipata choloŵera ku bwalo chija, panali nsalu zochinga, zotalika mamita asanu ndi aŵiri, zokhala ndi nsanamira zitatu ndi masinde atatu. Nsalu zonse zochinga kuzungulira bwalolo zinali za bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino. Masinde a nsanamirazo anali opangidwa ndi mkuŵa. Ndipo ngoŵe za pa nsanamirazo, mitanda yake ndi zokutira nsonga za nsanamirazo, zonsezo zinali zasiliva. Nsanamira zonse za bwalolo zidalumikizidwa ndi mitanda yasiliva. Nsalu zochingira pa chipata cha ku bwalolo, zokongoletsedwa ndi zopetapeta, zinali zobiriŵira, zofiirira ndi zofiira, ndiponso za bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino. Kutalika kwake kunali mamita asanu ndi anai, msinkhu wake unali masentimita 229 monga zochingira zake za bwalolo. Nsaluzo adazikoloŵeka ku nsanamira zinai zokhala m'masinde anai amkuŵa. Ngoŵe za pa nsanamira, mitu yake ndi mitanda yake, zonsezo zinali zasiliva. Koma zikhomo zake za chihema cha Chauta, ndiponso zikhomo zake za bwalolo, zonsezo zinali zamkuŵa. Nachi chiŵerengero cha golide, siliva ndi mkuŵa zimene ankazigwiritsa ntchito m'chihema chaumboni cha Chauta, monga momwe Mose adalamulira. Alevi ndiwo anali ndi udindo wakuziŵerenga, ndipo amene ankaŵatsogolera ndi Itamara, mwana wa wansembe Aroni. Ndipo Bezalele, mwana wa Uri, mdzukulu wa Huri, wa fuko la Yuda, adapanga zonse zimene Chauta adalamula Mose kuti apange. Mthandizi wake Oholiyabu, mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani, anali wodziŵa kuzokota miyala, kulemba mapulani, ndi kuwomba nsalu yopetedwa ndi thonje lobiriŵira, lofiirira ndi lofiira, ndiponso nsalu ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino. Golide yense amene ankagwiritsa ntchito popanga malo opatulika, anali golide amene anthu adaapereka kwa Chauta, ndipo ankalemera makilogaramu 1,000, potsata miyeso ya ku Nyumba ya Mulungu. Siliva wochokera kwa mpingo wonse wa anthu, anali wolemera makilogaramu 3,430, potsata miyeso ya ku Nyumba ya Mulungu. Munthu aliyense ankapereka beka imodzi (ndiye kuti magaramu ngati 6, potsata muyeso wa ku Nyumba ya Mulungu.) Anthu onse olembedwa m'kaundula analipo 603,550 amuna okha, a zaka makumi aŵiri kapena kupitirira. Siliva wolemera makilogaramu 3,400 adamangira masinde 100 a malo opatulika ndi a nsalu zochingira. Tsinde lililonse linkalira siliva wolemera makilogaramu 34. Ndi makilogaramu otsalawo adapanga ngoŵe za pa nsanamirazo ndipo adakuta nsonga za nsanamira ndi kupanga mitanda yake. Mkuŵa umene adaapereka kwa Chauta udakwana makilogaramu 2,425 pamodzi. Tsono ndi mkuŵa umenewu adapanga masinde a pa chipata choloŵera ku chihema chamsonkhano. Adapanganso guwa la nsembe zopsereza, pamodzi ndi chitsulo cha sefa, zipangizo zonse za guwalo, masinde a bwalo lonse lozungulira, ndi zikhomo zonse za chihema cha Chauta ndi za bwalo lonse lozungulira. Tsono adapanga zovala zokongola kwambiri za ansembe, zovala potumikira m'malo oyera. Adapanga zovalazo ndi nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira. Adapanga zovala za Aroni monga momwe Chauta adalamulira Mose. Adapanga chovala chopatulika cha efodi ndi nsalu yagolide ndiponso ndi nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndi ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino. Ndipo adasula golide mwaphanthiphanthi, namlenzalenza, kuti amlukire kumodzi ndi thonje lobiriŵira, lofiirira ndi lofiira, ndiponso la bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, ntchito yaumisiri. Tsono adapanga tizikwewo tam'mapewa ta chovala cha efodi chija, tolumikizika ku chovalacho pa mbali zake ziŵiri. Panalinso lamba woluka mwaluso, womangira efodi, wolukira kumodzi ndi efodiyo. Lambayo nayenso anali wa nsalu yagolide, ndi wa nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso wa bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino, monga momwe Chauta adalamulira Mose. Kenaka adakonza miyala yakongola ya mtundu wa onikisi, naikhazika m'zoikamo zake zagolide. Tsono adaizokota monga amachitira pa chidindo, nalembapo mozokota bwino maina onse a ana aamuna a Israele. Yonseyo adaiika pa tizikwewo tam'mapewa ta chovala cha efodi chija, kuti iziŵakumbutsa ana a Israele, monga momwe Chauta adalamulira Mose. Pambuyo pake adapanga chovala chapachifuwa mwaluso kwambiri, monga chovala cha efodi chija. Adachipanga ndi nsalu yagolide, ndi nsalu yobiriŵira, yofiirira, ndi yofiira, ndiponso ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino. Kutalika kwake kwa chovala chapachifuwacho kunali masentimita 23, muufupi mwakenso masentimita 23, ndipo chinali chopinda paŵiri. Tsono adaikapo mizere inai ya miyala yokongola. Pa mzere woyamba adaika miyala ya rubi, topazi ndi garaneti. Pa mzere wachiŵiri adaika miyala ya emeradi, safiro ndi daimondi. Pa mzere wachitatu adaika miyala ya opela, agate ndi ametisiti, ndipo pa mzere wachinai adaika miyala ya berili, onikisi ndi yasipara. Miyalayo adaiika m'zoikamo zagolide. Panali miyala khumi ndi iŵiri imene adalembapo maina a mafuko a Israele. Inali miyala khumi ndi iŵiri yozokotedwa ngati zidindo, ndipo mwala uliwonse unali ndi dzina la fuko limodzi. Adapanga timaunyolo ta chovala chapachifuwa ta golide wabwino kwambiri, topota mwaluso ngati maukufu. Adapanganso zoikamo zake ziŵiri zagolide zonga maluŵa, ndiponso mphete ziŵiri, ndipo adalumikiza mphete ziŵirizo ku nsonga zake zapamwamba za chovala chapachifuwacho. Tsono zingwe ziŵiri zagolide adazilumikiza ku mphete ziŵiri zija, ndi kulumikiza nsonga ziŵiri zina za zingwezo m'zoikamo zake ziŵiri zija. Motero adazilumikiza patsogolo pa tizikwewo tam'mapewa ta chovala cha efodi chija. Adapanga mphete ziŵiri zagolide, nazilumikiza ku nsonga ziŵiri za chovala chapachifuwa cham'mphepete, m'kati mwake, pafupi ndi chovala cha efodi chija. Adapanganso mphete ziŵiri zagolide, nazilumikiza ku mbali yam'munsi, kutsogolo kwa tizikwewo tam'mapewa ta chovala cha efodi chija, pafupi ndi msoko, ndiponso pamwamba pa lamba woluka mwaluso uja wa efodiyo. Ndipo adalumikiza mphete za chovala chapachifuwa zija ku mphete za efodi. Adalumikiza ndi kamkuzi kobiriŵira, kuti chovala chapachifuwacho chikhale pamwamba pa lamba woluka mwaluso uja, ndipo chisalekane ndi efodi ija, monga momwe Chauta adalamulira Mose. Adapanga mkanjo wake wa efodi, woombedwa ndi nsalu yobiriŵira. Mkanjowo unali ndi popisa mutu, ndipo maonekedwe ake anali ngati popisa mutu pa malaya. M'mbali mwake kuzungulira, munali mosokerera bwino, kuti ungang'ambike. Pa mpendero wake wapansi, adalumikizapo zithunzi za makangaza zopangidwa ndi nsalu yobiriŵira, yofiirira ndi yofiira, ndiponso ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino. Adapanganso timabelu ta golide wabwino kwambiri, mopakiza pakati pa makangazawo, kuzungulira mpendero wonse wam'munsiwo. Tsono panali khangaza limodzi ndi kabelu kamodzi, khangaza limodzi ndi kabelu kamodzi, kuzungulira mpendero wonse wa mkanjo, umene ansembe ankavala pogwira ntchito zaunsembe, monga momwe Chauta adalamulira Mose. Tsono Aroni ndi ana ake, amisiri aja adaŵapangira miinjiro, nduŵira, makofiya ndi akabudula, zonsezo zopangidwa ndi nsalu ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino. Adapanganso lamba wa bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino ndi wa thonje lobiriŵira, lofiira ndi lofiirira, ndipo adamkongoletsa ndi zopetapeta, monga momwe Chauta adalamulira Mose. Ndipo adapanga duŵa la golide wabwino kwambiri. Limenelo linali chizindikiro chopatulika, ndipo mofanizira ndi mazokotedwe a chidindo, adazokotapo mau akuti, “Chopereka kwa Chauta.” Kenaka adatenga kamkuzi kobiriŵira namangirira duŵa limenelo ku nsalu ya nduŵira ija, monga momwe Chauta adalamulira Mose. Tsono ntchito yonse yomanga chihema chamsonkhano idatha. Aisraele aja adachitadi zonse, monga momwe Chauta adalamulira Mose. Pambuyo pake zonsezo adabwera nazo kwa Mose: chihema chija chodzakhala Nyumba ya Mulungu, pamodzi ndi zipangizo zake zonse, ngoŵe zake zokoŵera, mafulemu ake, mitanda yake, nsanamira zake ndi masinde ake omwe. Adabweranso ndi chophimbira cha chikopa chankhosa chonyika mu utoto wofiira, chophimbira cha chikopa chambuzi, nsalu zochingira, bokosi loikamo miyala yaumboni pamodzi ndi nsanamira zake, ndiponso chivundikiro cha bokosilo. Adabweranso ndi tebulo, pamodzi ndi zipangizo zake, ndipo adaika buledi woperekedwa kosalekeza kwa Mulungu; choikaponyale cha golide wabwino kwambiri, nyale zake pamodzi ndi zipangizo zake, mafuta anyale; guwa lagolide, mafuta odzozera, lubani wa fungo lokoma, nsalu yotsekera pa chipata choloŵera m'chihema, guwa lamkuŵa, pamodzi ndi chitsulo cha sefa, mphiko zake, pamodzi ndi zipangizo zake zonse, ndiponso beseni losambira ndi phaka lake. Adabweranso ndi nsalu zochingira bwalo pamodzi ndi nsanamira zake ndi masinde ake, nsalu yochingira pa chipata choloŵera m'bwalolo, pamodzi ndi zingwe zake ndi zikhomo zake, ndiponso zipangizo zonse zotumikira nazo m'chihema cha Chauta chija. Adabweranso ndi zovala zokongola kwambiri zoyenera kuvala ansembe potumikira m'malo oyera, zovala zopatulika za wansembe Aroni, ndiponso zovala za ana ake aamuna, zoyenera kuzivala pogwira ntchito zaunsembe. Motero Aisraele adachitadi ntchito zonse, monga momwe Chauta adalamulira Mose. Tsono Mose adaona zonse zimene zidapangidwazo, ndipo adatsimikiza kuti adazipangadi monga momwe Chauta adalamulira. Pamenepo Mose adaŵadalitsa anthu onsewo. Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, uutse chihema chamsonkhano. Bokosi m'mene muli miyala yaumboni uliike m'menemo, ndipo bokosilo uliphimbe ndi nsalu kuti ulichinge. Ukhazikemonso tebulo, pamwamba pake uikepo zipangizo zake, ndipo uikemo choikaponyale ndi nyale zake. Tsono uike guwa lagolide lofukizirapo lubani patsogolo pa bokosi laumboni. Pa chipata cha Nyumba ya Mulungu utsekepo ndi nsalu zochinga. Uike guwa lootcherapo nsembe patsogolo pa chihema chamsonkhanocho. Beseni uliike pakati pa chihema chamsonkhano ndi guwa, ndipo uthiremo madzi. Upange bwalo kuzungulira chihemacho, ndi kukoloŵeka nsalu zochingira pa chipata chake cha bwalolo. “Pambuyo pake utenge mafuta odzozera aja, udzoze Nyumba ya Mulungu ndi zonse za m'menemo. Uipereke kwa Mulungu Nyumbayo, pamodzi ndi zipangizo zake zonse, kuti idzakhale yoyera. Tsono udzozenso guwa loperekapo nsembe zopsereza, pamodzi ndi zipangizo zake zomwe. Guwalo ulipereke kwa Mulungu, kuti likhale loyera ndipo lidzakhaladi loyera kopambana. Udzoze beseni losambira, pamodzi ndi phaka lake lomwe, ndipo ulipereke kwa Mulungu, kuti likhale loyera. “Pambuyo pake ubwere ndi Aroni ku chipata cha chihema chamsonkhano, pamodzi ndi ana ake omwe, ndipo onsewo asambe kumeneko. Aroniyo umuveke zovala zopatulika. Umdzoze, ndipo umpatule kuti akhale wansembe wonditumikira Ine. Ana ake abwerenso, ndipo uŵaveke miinjiro. Tsono uŵadzoze monga momwe udadzozera bambo wao, kuti akhale ansembe onditumikira Ine. Kudzozedwako kudzaŵasandutsa ansembe pa mibabwo ndi mibadwo.” Mose adachita zonse, monga momwe Chauta adamlamulira. Motero pa tsiku loyamba la mwezi woyamba chaka chachiŵiri, malo opatulika adautsidwa. Poutsa malowo, Mose adakhazika masinde ake pansi, ndipo adautsa mafulemu ake, nalumikiza mitanda yake, nautsanso nsanamira zake zija. Pambuyo pake adautsa chihema pamwamba pa malo opatulikawo, nachiphimba ndi chophimbira chake cha chihema, monga momwe Chauta adamlamulira. Tsono adatenga miyala yaumboni ija naiika m'bokosi muja. Adapisa mphiko zija m'mphete za bokosilo, naika chivundikiro pamwamba pake. Kenaka adaika bokosilo m'malo opatulika, ndipo adaika nsalu zochingira. Motero adachinga bokosi laumboni, monga momwe Chauta adamlamulira. Tsono m'chihema chamsonkhanomo adaikamo tebulo, chakumpoto kwa malo opatulika, kunja kwa nsalu yochinga ija, ndipo pamwamba pa tebulolo adaikapo buledi, monga momwe Chauta adamlamulira. M'chihema chamsonkanomo adaikamo choikaponyale mopenyana ndi tebulo chakumwera kwake kwa malo opatulika. Tsono pa choikaponyalecho adaikapo nyale, kuti zikhale pamaso pa Chauta, monga momwe Iye adalamulira Mose. M'chihema chamsonkhanomo adaikamo guwa lagolide patsogolo pa nsalu yochinga. Adafukiza lubani wa fungo lokoma paguwapo, monga momwe Chauta adamlamulira. Pa khomo la malo opatulika adaikapo nsalu yochinga. Ndipo adaika guwa la nsembe zopsereza pa khomo la chihema chamsonkhano. Pa guwa limenelo adaperekapo nsembe zopsereza ndiponso chopereka cha chakudya, monga momwe Chauta adamlamulira. Kenaka adaika beseni losambira lija pakati pa chihema chamsonkano ndi guwa, nathiramo madzi osamba. Apo Mose, Aroni ndi ana ake adasamba m'manja natsuka mapazi ao. Nthaŵi zonse akaloŵa m'chihema chamsonkhanomo, kapena kusendera ku guwalo, ankasamba, monga momwe Chauta adalamulira Mose. Adamanga bwalo lonse lozungulira chihema chija ndi guwa. Adaikanso nsalu yochinga pa chipata cha bwalolo. Motero Mose adamaliza ntchito yonseyo. Mtambo udaphimba chihema chamsonkhanocho, ndipo ulemerero wa Chauta udachidzaza Mose sadathe kuloŵa m'chihema chamsonkhanocho chifukwa mtambo unali momwemo, ndipo ulemerero wa Chauta udaadzaza chihema chake. Pa maulendo ao onse, mtambo ukachoka pachihemapo, Aisraelewo ankachoka pamene analiripo. Koma mtambowo ukapanda kuchoka, Aisraele sankachokanso pachigonopo. Ankadikira tsiku lakuti mtambo wachokapo. Unkakhala pachihemapo masana, usiku mumtambomo munkayaka moto, ndipo Aisraele onse ankatha kuupenya. Zinkatero pa ulendo wao wonse. Pamene Chauta anali m'chihema chamsonkhano adaitana Mose, namuuza kuti, “Uza Aisraele kuti, ‘Munthu aliyense akamabwera ndi chopereka kwa Chauta, azitenga ng'ombe kapena nkhosa kapena mbuzi.’ “Ngati munthu apereka nsembe yopsereza kwathunthu, azipereka ng'ombe yamphongo yopanda chilema. Aziiperekera pa khomo la chihema chamsonkhano, kuti Chauta ailandire. Tsono asanjike dzanja lake pamutu pa ng'ombeyo, ndipo idzalandiridwa kuti ikhale yopepesera machimo ake. Pambuyo pake aiphe pamaso pa Chauta, ndipo ansembe, ana a Aroni, abwere ndi magazi ake. Awaze magaziwo mozungulira guwa limene lili pa khomo la chihema chamsonkhano. Ndipo asende nyamayo ndi kuidula nthulinthuli. Tsono ansembe, ana a Aroni aja, asonkhe moto pa guwa, ndipo ayalike nkhuni pamotopo. Pamenepo ansembe aike nthuli za nyamayo, mutu wake pamodzi ndi mafuta omwe, pa nkhuni zimene zili pa guwalo. Koma atsuke matumbo ake pamodzi ndi miyendo yake yomwe. Tsono wansembe aipsereze nyama yathunthuyo pa guwa, kuti ikhale nsembe yopsereza, yotentha pa moto, ya fungo lokomera Chauta. “Ngati munthu apereka nsembe yopsereza ya nkhosa kapena mbuzi, ikhale yaimuna yopanda chilema. Ndipo aiphere cha kumpoto kwa guwa, pamaso pa Chauta. Tsono ansembe, ana a Aroni, awaze magazi ake pa guwalo molizungulira. Pambuyo pake ataidula nthulinthuli nyamayo, atengenso mutu ndi mafuta omwe, ndipo aike zonsezo pa nkhuni zimene zili pa guwa. Koma matumbo ake aŵatsukire padera, pamodzi ndi miyendo yake yomwe. Ndipo wansembe apereke zonsezo ndi kuzitentha pa guwa. Imeneyo ndiyo nsembe yopsereza, yotentha pa moto, ya fungo lokomera Chauta. Ngati munthu apereka kwa Chauta nsembe yopsereza ya mbalame, ikhale njiŵa kapena nkhunda. Wansembe abwere nayo ku guwa, aidule mutu moipotola, ndi kutentha mutuwo paguwapo. Magazi ake aŵathire pansi kuti ayenderere pambali pa guwa. Tsono achotse chitsokomero pamodzi ndi nthenga zake zomwe, ndi kuzitaya potayira phulusa, pafupi ndi guwa, cha kuvuma kwake. Pambuyo pake aing'ambe pakati, phiko lina uku, lina uku, koma osachotsa mapikowo. Kenaka aitenthe pa moto wankhuni wapaguwa. Imeneyo ndiyo nsembe yopsereza, yotentha pa moto, ya fungo lokomera Chauta. “Munthu wina aliyense akabwera kudzapereka chopereka cha chakudya kwa Chauta, nsembeyo ikhale ya ufa wosalala. Ufawo authire mafuta ndi lubani, ndipo abwere nawo kwa ansembe, ana a Aroni. Atapeko ufa wosakaniza ndi mafuta uja dzanja limodzi, ndi lubani wake yense. Tsono wansembe atenthe zimenezo pa guwa, kusonyeza kuti nsembeyo yaperekedwa kwa Chauta, ndi nsembe yotentha pa moto, ya fungo lokomera Chauta. Zotsala za chopereka cha chakudyacho zikhale za Aroni pamodzi ndi ana ake. Chimenecho ndicho chigawo chopatulika kopambana, chifukwa chatapidwa pa nsembe yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta. “Ukamapereka chopereka cha chakudya chophika mu uvuni, chikhale buledi wa ufa wa tirigu wosalala wopanda chofufumitsira, wosakaniza ndi mafuta, kapena ikhale timitanda ta buledi wosafufumitsa, topyapyala, topaka mafuta. Nsembe yako ikakhala chakudya chophika pa chitsulo chamoto, chikhale buledi wa ufa wosalala wopanda chofufumitsira, wosakaniza ndi mafuta. Umuduledule ndi kumupaka mafuta. Chimenecho ndicho chopereka cha chakudya. Ndipo nsembe yako ikakhala ya chopereka cha chakudya chophika pa chiwaya, chikhale ya ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. Tsono ubwere nacho chopereka chimenechi kwa Chauta, ndipo utachipereka kwa wansembe, iyeyo abwere nacho ku guwa. Apo wansembeyo atengeko gawo lina la choperekacho kusonyeza kuti chaperekedwa kwa Chauta, tsono achitenthe paguwapo. Imeneyo ndiyo nsembe yotentha pa moto, ya fungo lokomera Chauta. Ndipo zotsala za chopereka cha chakudyacho zikhale za Aroni ndi ana ake. Chimenecho ndicho chigawo chopatulika kopambana, chifukwa chatapidwa pa nsembe yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta. “Chopereka cha chakudya chimene upereka kwa Chauta chikhale chopanda chofufumitsira, pakuti suyenera kupereka kwa Chauta nsembe yotentha pa moto, imene ili ndi chofufumitsira kapena uchi. Ziŵirizo ungathe kubwera nazo ngati nsembe ya zokolola zoyambirira zopereka kwa Chauta. Koma usazitenthere pa guwa kuti zipereke fungo lonunkhira. Zopereka zako zonse za zakudya uzithire mchere, osaiŵala ai: mcherewo ndi wosonyeza chipangano cha pakati pa iwe ndi Mulungu wako. Uzithira mchere nsembe zako zonse. “Ukamapereka kwa Chauta chopereka cha chakudya choyamba kucha, nsembeyo ikhale ya mbeu zatsopano zokazinga ndi zopunthapuntha. Ndipo uchithithire mafuta ndi lubani. Chimenecho ndicho chopereka cha chakudya. Tsono wansembe atenthe chigawo cha mbeu zopunthapuntha zija ndi cha mafuta, ndiponso lubani wake yense, kuti ikhale nsembe yachikumbutso. Imeneyo ndiyo nsembe yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta. “Ngati munthu apereka nsembe yachiyanjano kwa Chauta, nsembe yake ikakhala ya ng'ombe yamphongo kapena yaikazi, ikhale yopanda chilema. Munthuyo asanjike dzanja lake pamutu pa ng'ombeyo, ndipo aiphere pa khomo la chihema chamsonkhano. Pomwepo ansembe, ana a Aroni, aliwaze magazi guwa molizungulira. Ndipo pa nsembe yachiyanjanoyo, yopereka kwa Chauta ndi yoyenera kuitentha pa moto, atapepo mafuta okuta matumbo. Apatulenso imso ziŵiri, pamodzi ndi mafuta ake omwe, ndiponso mphumphu ya mafuta akuchiŵindi, ochotsa pamodzi ndi imso zija. Tsono ana a Aroni atenthe zonsezo pa guwa, pamodzi ndi nsembe yopsereza imene ili pa nkhuni pamotopo. Imeneyo ndiyo nsembe yotentha pa moto, ya fungo lokomera Chauta. “Ngati munthu apereka nsembe yachiyanjano kwa Chauta, nsembe yake ikakhala nkhosa yamphongo kapena yaikazi, ikhale yopanda chilema. Akapereka nkhosa kuti ikhale nsembe, abwere nayo pamaso pa Chauta. Asanjike dzanja lake pamutu pa nkhosayo, ndipo aiphere pa khomo la chihema chamsonkhano. Pambuyo pake ana a Aroni aliwaze magazi guwa molizungulira. Tsono pa nsembe yachiyanjanoyo yopereka kwa Chauta ndi yoyenera kuitentha pa moto, atapepo mafuta onse a nkhosayo, ndiye kuti mchira wonona wathunthu, ataudula m'tsinde pafupi ndi msana, mafuta okuta matumbo, mafuta ena onse okhala pamatumbopo, impso ziŵiri pamodzi ndi mafuta ake omwe, ndiponso mphumphu ya mafuta akuchiŵindi, ochotsa pamodzi ndi imso zija. Tsono wansembe atenthe zonsezo pa guwa, kuti zikhale chakudya chotentha pa moto, chopereka kwa Chauta. “Ngati munthu akuti apereke mbuzi, abwere nayo pamaso pa Chauta. Asanjike dzanja lake pamutu pa mbuziyo, ndipo aiphere pakhomo pa chihema chamsonkhano. Pambuyo pake ana a Aroni aliwaze magazi guwa molizungulira. Tsono pa nsembe yopereka kwa Chautayo ndipo yoyenera kuitentha pa moto, atapepo mafuta okuta matumbo ndi mafuta ena onse okhala pamatumbopo. Apatulenso imso ziŵiri pamodzi ndi mafuta ake omwe cham'chiwunomu, ndiponso mphumphu ya mafuta akuchiŵindi, ochotsa pamodzi ndi imso zija. Wansembe atenthe zonsezo pa guwa, kuti zikhale chakudya chotentha pa moto, cha fungo lokoma. Mafuta onse nga Chauta. Limeneli likhale lamulo lamuyaya pa mibadwo yanu yonse, kuti musadzadye mafuta kapena magazi kulikonse kumene mudzakhale.” Chauta adauza Mose kuti, “Uza Aisraele kuti pa zonse zimene Chauta adaletsa, munthu aliyense akachimwapo mosadziŵa, pochita kanthu kena kalikonse koletsedwa, azichita izi: wochimwayo akakhala wansembe wodzozedwa, pakutero wausandutsa wopalamula mpingo wonse, tsono azipereka kwa Chauta ng'ombe yaing'ono yamphongo yopanda chilema, chifukwa cha tchimo lakelo. Imeneyo ndiyo nsembe yopepesera machimo ake. Wansembe abwere ndi ng'ombeyo pa khomo la chihema chamsonkhano pamaso pa Chauta. Tsono asanjike dzanja lake pamutu pa ng'ombeyo, ndipo aiphe pamaso pa Chauta. Kenaka wansembe wodzozedwayo atengeko magazi a ng'ombeyo ndi kubwera nawo ku chihema chamsonkhano. Apo aviike chala chake m'magazi, ndi kuwaza magaziwo kasanu ndi kaŵiri patsogolo pa nsalu yochinga malo oyera pamaso pa Chauta. Pambuyo pake wansembe apakeko magaziwo pa nyanga za guwa la m'chihema chamsonkhano lofukizirapo lubani wonunkhira fungo lokoma pamaso pa Chauta. Magazi ena otsala a ng'ombeyo aŵathire pa tsinde la guwa la nsembe zopsereza, limene lili pa khomo la chihema chamsonkhano. Tsono mafuta onse a ng'ombe yamphongo yoperekera nsembe yopepesera machimoyo, aŵachotse pamodzi ndi mafuta okuta matumbo, ndiponso mafuta ena onse okhala pamatumbopo. Achotsenso imso ziŵiri pamodzi ndi mafuta ake omwe cham'chiwunomu, ndiponso mphumphu za mafuta akuchiŵindi ochotsa pamodzi ndi imso zija, monga momwe amazichotsera ku ng'ombe yopereka pa nsembe yachiyanjano. Tsono wansembeyo atenthe zonsezo pa guwa la nsembe zopsereza. Koma chikopa cha ng'ombe yamphongoyo, pamodzi ndi mnofu wake, mutu wake, miyendo yake, matumbo ake ndi ndoŵe yake, kungoti ng'ombe yonseyo, atuluke nayo kunja kwa mahema, ku malo oyeretsedwa kumene amatayako phulusa, ndipo pamalo pomwepo aitenthere pa moto wankhuni. “Ngati mpingo wonse wa Aisraele uchimwa mosachitira dala, nuchita zimene Chauta amaletsa, ngakhale uli wosadziŵako, ngwopalamula ndithu. Tsono tchimo lakelo nkudziŵika, mpingo wonsewo upereke ng'ombe yaing'ono yamphongo kuti ikhale nsembe yopepesera machimo, ndipo abwere nayo pa khomo la chihema chamsonkhano. Apo atsogoleri a mpingo asanjike manja ao pamutu pa ng'ombe yamphongoyo pamaso pa Chauta, ndipo aiphe pamaso pa Chauta. Wansembe wodzozedwa atengeko magazi a ng'ombe yamphongoyo ndi kubwera nawo ku chihema chamsonkhano. Pamenepo wansembeyo aviike chala chake m'magazi, ndipo pamaso pa Chauta awaze magaziwo kasanu ndi kaŵiri patsogolo pa nsalu yochinga. Pambuyo pake magaziwo aŵapake pa nyanga za guwa limene lili m'chihema chamsonkhano pamaso pa Chauta. Magazi ena otsala aŵathire patsinde pa guwa la nsembe zopsereza, limene lili pa khomo la chihema chamsonkhano. Kenaka mafuta ake onse aŵachotse ndi kuŵatenthera pa guwa. Umu ndimo m'mene ng'ombe yamphongo aichitire. Monga adachitira ndi ng'ombe yamphongo yopereka pa nsembe yopepesera machimo, ndimo aichitirenso imeneyi. Wansembeyo atachita mwambo wopepesera machimowu, mpingowo udzakhululukidwa. Tsono ng'ombeyo aitulutsire kunja kwa mahema ndi kuitentha monga momwe adachitira ndi yoyamba ija. Imeneyo ndiyo nsembe yopepesera machimo, yoperekera mpingo wonse. “Wolamula akachimwa mosadziŵa, kuchimwira Chauta, Mulungu wake, pa chinthu choletsedwa, napalamula pakutero, pambuyo pake ena nkumudziŵitsa za tchimo lakelo, iyeyo apereke nsembe ya tonde wopanda chilema. Tsono wolamulayo asanjike dzanja lake pamutu pa tondeyo ndi kumupha pamalo pomwe amaphera nsembe yopsereza pamaso pa Chauta. Imeneyo ndiyo nsembe yopepesera machimo. Wansembe atengeko magazi a tondeyo ndi chala chake, aŵapake pa nyanga za guwa la nsembe zopsereza, ndi kuthira magazi otsalowo patsinde pa guwa lomwelo. Kenaka mafuta ake onse aŵatenthere pa guwa, monga momwe amachitira ndi mafuta a nsembe yachiyanjano. Wansembeyo atachita mwambo wopepesera machimo a wopalamula uja, munthuyo adzakhululukidwa. “Ngati munthu wamba aliyense achimwa mosadziŵa, pochita china chilichonse chimene Chauta amaletsa, napalamula pakutero, tchimo lakelo akalizindikira, apereke nsembe ya mbuzi yaikazi yopanda chilema, chifukwa cha tchimo lakelo. Tsono asanjike dzanja lake pamutu pa mbuzi ya nsembe yopepesera machimoyo, ndipo aiphere pa malo amene amaperekera nsembe yopsereza. Atatero, wansembe atengeko magazi ndi chala chake, ndi kuŵapaka pa nyanga za guwa la nsembe zopsereza, ndipo magazi otsalawo aŵathire patsinde pa guwa lomwelo. Tsono achotse mafuta ake onse, monga momwe amachotsera mafuta a nsembe yachiyanjano, ndipo wansembe aŵatenthe pa guwalo, kuti atulutse fungo lokomera Chauta. Wansembeyo atachita mwambo wopepesera machimo a munthu wamba uja, munthuyo adzakhululukidwa. “Ngati munthu abwera kudzapereka nkhosa ya nsembe yopepesera machimo, nkhosa yake ikhale yaikazi, yopanda chilema. Ndipo asanjike dzanja lake pamutu pa nkhosa ya nsembe yopepesera machimoyo, ndi kuiphera pa malo amene amaphera nsembe yopsereza. Pambuyo pake wansembe atengeko magazi a nkhosayo ndi chala chake, ndipo aŵapake pa nyanga za guwa la nsembe zopsereza, ndi kuthira magazi otsalawo patsinde pa guwalo. Tsono achotse mafuta ake onse, monga momwe amachotsera mafuta a nkhosa yoperekera nsembe yachiyanjano. Ndipo aŵatenthe pa guwa, pamodzi ndi nsembe zina zopsereza pa moto, zopereka kwa Chauta. Umu ndimo m'mene wansembe azichitira mwambo wopepesera tchimo la munthu, ndipo munthuyo adzakhululukidwa. “Munthu akaitanidwa ku bwalo la milandu, namlumbiritsa kuti achite umboni wa zinthu zimene adaziwona kapena adazidziŵa, iyeyo nakana kupereka umboniwo, munthu ameneyo ndi woyenera kumlanga. Munthu akakhudza chinthu chilichonse chonyansa pa zachipembedzo, monga nyama yakufa yam'thengo kapena yoŵeta, kapenanso zokwaŵa zakufa, ndipo pokhudzapo adziipitsa mosadziŵa, munthu ameneyo ndi woipitsidwa, ndiponso ndi wopalamula. Wina aliyense akakhudza zonyansa za munthu za mtundu uliwonse, ndipo pokhudzapo adziipitsa mosadziŵa, munthu ameneyo akhala wopalamula, akangozindikira pambuyo pake zimene wachita. Munthu akalakwa polumbira mofulumira kuti adzachita chinthu choipa kapena chabwino, kulumbira kwake kwa mtundu uliwonse kumene anthu amachita, ndipo polumbirapo sadziŵa vuto lake, munthu ameneyo akhala wopalamula, akangozindikira pambuyo pake zimene wachita. Munthu akapalamula pa chilichonse mwa zimene tatchulazi, aulule tchimo lakelo. Kenaka abwere kudzapereka nsembe kwa Chauta, chifukwa cha tchimo lakelo. Nsembe yake ikhale ya nkhosa yaikazi kapena ya mbuzi yaikazi. Tsono wansembe achite mwambo wopepesera machimo a wopalamula uja. “Koma ngati munthu alibe nkhosa kapena mbuzi, atenge njiŵa ziŵiri kapena nkhunda ziŵiri, kuti zikhale nsembe yopereka kwa Chauta yopepesera machimo ake. Imodzi ikhale nsembe yopepesera machimo, ndipo inayo ikhale nsembe yopsereza. Abwere nazo kwa wansembe, ndipo wansembeyo ayambe wapereka mbalame yopepesera machimoyo. Aipotole khosi, koma asaidule mutu, ndipo awazeko magazi a mbalameyo m'mbali mwa guwa. Koma magazi ena otsala aŵathire pansi, kuti ayenderere patsinde pa guwalo. Imeneyo ndiyo nsembe yopepesera machimo. Ndipo apereke mbalame inayo kuti ikhale nsembe yopsereza, potsata mwambo wake. Wansembe atachita mwambo wopepesera machimo amene munthuyo wachita, wochimwayo adzakhululukidwa. “Ngati munthu alibe njiŵa ziŵiri kapena nkhunda ziŵiri, abwere ndi ufa wosalala wokwanira muyeso wa kilogaramu limodzi, kuti ukhale nsembe yopepesera tchimo limene wachita. Asathireko mafuta kapenanso lubani, chifukwa imeneyi ndi nsembe yopepesera machimo. Tsono abwere ndi ufa kwa wansembe, ndipo wansembeyo atapeko wa dzanja limodzi ngati chikumbutso ndi kuutenthera pa guwa, pamodzi ndi nsembe zopereka kwa Chauta. Imeneyi ndiyo nsembe yopepesera machimo. Umu ndimo m'mene wansembe adzachitire mwambo wopepesera munthu amene adachimwa, ndipo munthuyo adzakhululukidwa. Tsono zotsala zikhale za wansembeyo, monga momwe amachitira ndi chopereka cha chakudya.” Chauta adauza Mose kuti, “Munthu akachita zinthu mosakhulupirika, nachimwa posapereka kwa Chauta zinthu zopatulika zofunika, koma mosadziŵa, apereke kwa Chauta nsembe yopepesera kupalamula chifukwa cha tchimo lakelo. Nsembe yake ikhale nkhosa yamphongo yopanda chilema, ndipo mtengo wake wa nkhosayo udzakhale wokwana masekeli asiliva, potsata kaŵerengedwe ka ku Nyumba ya Mulungu. Imeneyo ndiyo nsembe yopepesera kupalamula. Tsono munthuyo abweze zopatulika zimene sadaperekezo, ndipo aonjezepo chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse, ndipo azipereka kwa wansembe. Apo wansembeyo adzachita mwambo wopepesera machimo a munthuyo, popereka nsembe yopepesera kupalamula ya nkhosa yamphongo ija, ndipo munthuyo adzakhululukidwa. “Munthu akachimwa pochita mosadziŵa zimene Chauta amaletsa, ndi wopalamulabe ndithu ameneyo, ndipo ndi woyenera kumlanga. Abwere kwa wansembe ndi nkhosa yamphongo yopanda chilema, imene mtengo wake ulingane ndi wa nyama ya nsembe yopepesera kupalamula. Wansembeyo achite mwambo wopepesera machimo amene munthuyo adachita mosadziŵawo, ndipo wochimwayo adzakhululukidwa. Imeneyo ndiyo nsembe yopepesera kupalamula, chifukwa munthuyo ndi wopalamula pamaso pa Chauta.” Chauta adauza Mose kuti, “Munthu akachita zinthu mosakhulupirika, nachimwira Chauta chifukwa cha kunyenga mnzake pomakana kumubwezera mnzakeyo zimene adamsungiza, kapena kumubera, kapena kumnyenga, kapena kunama kuti sadatole zimene zidatayika, kapena kumalumbira zonama pa kanthu kalikonse, munthu akachimwa pa zimenezi ndi wopalamula ndithu, abweze zimene adalandazo, zimene adatenga monyengazo, zomsungizazo, ndi zotayika zimene adatolazo. Pa tsiku limene apezeke kuti wapalamuladi, abweze zonsezo ndi kuwonjezapo chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse, tsono amubwezere mwini wakeyo. Ndipo nsembe yopepesera kupalamula, yopereka kwa Chauta, abwere nayo kwa wansembe. Ikhale nkhosa yamphongo yopanda chilema, mtengo wake wa nkhosayo ukhale wokwanira mtengo woikidwa wa nyama ya nsembe yopepesera kupalamula. Tsono wansembe achite mwambo wopepesera machimo a munthuyo pamaso pa Chauta, ndipo zonse zimene wochimwayo adachita napalamula pakutero, zidzakhululukidwa.” Chauta adauza Mose kuti, “Ulamule Aroni pamodzi ndi ana ake kuti, ‘Lamulo la nsembe yopsereza kwathunthu ndi ili: nsembeyo izikhala pa moto pa guwa usiku wonse mpaka m'maŵa, ndipo moto wapaguwapowo uzikhala uli chiyakire. Tsono wansembe avale mkanjo wake wabafuta, avalenso kabudula wabafuta, ndipo atengeko phulusa la nyama yopsereza pa guwa ndi kulithira pambali pa guwa lomwelo. Tsono avule zovala zake, avale zina, ndipo aole phulusalo nkukaliika pa malo oyeretsedwa kunja kwa mahema. Moto wapaguwa uzikhala uli chiyakire, usazime. Wansembe azisonkhezera motowo ndi nkhuni m'maŵa mulimonse, ndipo aziyala nsembe yopsereza paguwapo, ndi kupserezapo mafuta a nsembe zachiyanjano. Moto ukhale uli chiyakire paguwapo, usazime.’ ” “Lamulo la chopereka cha chakudya ndi ili: ana a Aroni aipereke nsembeyo pamaso pa Chauta patsogolo pa guwa. Tsono mmodzi atapeko dzanja limodzi la ufa wosalala woperekedwa ku nsembeyo, pamodzi ndi mafuta ndi lubani yense amene ali pa chopereka cha chakudyacho. Azitenthe pa guwa, kuti zikhale chikumbutso, ndipo zitulutse fungo lokomera Chauta. Tsono Aroni ndi ana ake adye zimene zatsalapo. Zikhale zosafufumitsa, ndipo azidyere pa malo oyera, ndiye kuti pa bwalo la chihema chamsonkhano. Poziphika asathiremo chofufumitsira. Ndaŵapatsa zotsalazo kuti zikhale gawo lao la nsembe zanga zopsereza. Zonsezo nzoyera kwambiri monga nsembe yopepesera machimo, ndiponso nsembe yopepesera kupalamula. Ana onse aamuna a Aroni azidyako za nsembe zopsereza zopereka kwa Chauta, monga kudalembedwa kuti zidzatero nthaŵi zonse pa mibadwo yanu yonse. Chilichonse chimene chidzakhudze guwalo chidzaonongedwa chifukwa cha mphamvu ya kuyera kwake.” Chauta adauza Mose kuti, “Nsembe imene Aroni ndi ana ake ayenera kupereka kwa Chauta pa tsiku limene wansembe adzozedwa, izikhala yotere: apereke ufa wosalala wokwanira kilogaramu limodzi ngati chopereka cha chakudya cha nthaŵi zonse. Apereke theka limodzi m'maŵa, ndipo linalo apereke madzulo. Ipangidwe ndi mafuta pa chiwaya. Ubwere nacho ili yosakaniza bwino, yophikidwa mitandamitanda monga amachitira ndi chopereka cha chakudya. Ndipo aipereke kuti itulutse fungo lokomera Chauta. Tsono wansembe wa fuko la Aroni amene wadzozedwa kuti aloŵe m'malo mwake, aipereke kwa Chauta nthaŵi zonse monga kudalembedwera. Aipsereze nsembe yonse poti lamulo ndi lamuyaya. Chopereka cha chakudya chilichonse cha wansembe chikhale chopsereza kwathunthu, asachidye ai.” Chauta adauza Mose kuti, “Uza Aroni ndi ana ake kuti, ‘Lamulo la nsembe yopepesera machimo ndi ili: pamalo pomwe amaphera nsembe yopsereza, aphereponso nsembe yopepesera machimo kwa Chauta. Imeneyo ndi nsembe yoyera kopambana. Wansembe amene aiperekere machimoyo, adye nyamayo. Aidyere pa malo oyera, pa bwalo la chihema chamsonkhano. Aliyense wokhudza nsembeyo adzaonongedwa chifukwa cha mphamvu ya kuyera kwake. Tsono magazi ake akagwera pa chovala, muchape chovalacho pa malo oyera. Ndipo auphwanye mphika wadothi umene adaphikamo nyamayo. Koma akaphika wamkuŵa, autsuke mphikawo ndi kuutsukuluza ndi madzi. Munthu wamwamuna aliyense wa m'banja la ansembe angathe kudyako. Imeneyo ndiyo nsembe yoyera kopambana. Koma asadye nyama ya nsembe yopepesera machimo imene magazi ake amabwera nawo ku chihema chamsonkhano, kudzapepesera machimo ku malo oyera. Aitenthe pa moto imeneyo.’ “Nsembe yopepesera kupalamula njoyera kopambana. Lamulo lake ndi ili: pamalo pomwe amaphera nsembe yopsereza, azipheraponso nsembe yopepesera kupalamula, ndipo awaze magazi ake pa guwa mozungulira. Tsono apereke mafuta ake onse, mchira wamafuta ndi mafuta okuta matumbo. Aperekenso imso ziŵiri pamodzi ndi mafuta ake omwe cham'chiwunomu, ndiponso mphumphu ya mafuta akuchiŵindi ochotsa ndi imso zija. Wansembe azitenthere pa guwa zonsezo, kuti zikhale nsembe yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta. Imeneyo ndiyo nsembe yopepesera kupalamula. Munthu wamwamuna aliyense wa m'banja la ansembe angathe kudyako. Aidyere pa malo oyera. Imeneyo ndiyo nsembe yoyera kopambana. Nsembe yopepesera kupalamula njofanafana ndi nsembe yopepesera machimo, ndipo nsembe ziŵiri zonsezo zili ndi lamulo limodzi lokha. Wansembe wochita mwambo wopepesera machimo ndiye amene nyamayo ikhale yake. Ndipo wansembe wopereka nsembe yopsereza ya munthu wina aliyense, atenge chikopa cha nsembe yopserezayo kuti chikhale chake. Tsono chopereka chilichonse cha chakudya chophika mu uvuni, kapena cha zonse zimene amakazinga mu mphika kapena m'chiwaya, zikhale za wansembe amene apereke zimenezo. Ndipo chopereka chilichonse cha chakudya chosakaniza ndi mafuta kapena chouma, chikhale cha ana onse a Aroni. Anawo aigaŵane molingana. “Lamulo la nsembe yachiyanjano imene aliyense angathe kupereka kwa Chauta ndi ili: akaipereka chifukwa cha kuthokoza, pamodzi ndi nsembe yothokozerayo apereke makeke osafufumitsa, osakaniza ndi mafuta, timitanda ta buledi wosafufumitsa, topyapyala, topaka mafuta, ndiponso makeke a ufa wosalala wosakaniza bwino ndi mafuta. Pamodzi ndi nsembe yachiyanjano yothokozerayo, abwere ndi mitanda ya buledi wotupitsa. Kenaka atengeko mtanda umodzi pa mtundu uliwonse wa buledi, kuti ukhale nsembe yopereka kwa Chauta. Mtanda umenewo ndi wake wa wansembe amene awaze magazi a nsembe zachiyanjano. Nyama ya nsembe yachiyanjano yothokozerayo aidye pa tsiku lopereka nsembe yakeyo. Asaisungeko mpang'ono pomwe kufikira m'maŵa mwake. Koma nsembe yake ikakhala yoti waipereka moilumbirira kapena mwaufulu, aidye pa tsiku lomwe akuiperekalo, ndipo nyama yotsala aidye m'maŵa mwake. Koma nyama yotsalako kufikira tsiku lachitatu, aitenthe pa moto. Ngati munthu adya nyama ya nsembe yachiyanjano pa tsiku lachitatu, amene waiperekayo Mulungu sadzamulandira, ndipo nsembeyo sidzampindulira kanthu. Idzakhala chinthu chonyansa ndipo amene adzadye imeneyo adzakhala wopalamula. “Nyama imene ikhudza chinthu chilichonse chonyansa pa zachipembedzo, munthu asaidye, koma itenthedwe pa moto. Onse amene ali osaipitsidwa pa zachipembedzo angathe kudya nyama ya nsembe. Koma munthu woipitsidwa akadya nyama ya nsembe yachiyanjano yopereka kwa Chauta, achotsedwe pakati pa Aisraele anzake. Ndipo wina aliyense akakhudza chinthu chonyansa pa zachipembedzo, kaya nchonyansa cha munthu kapena cha nyama, kapenanso chonyansa china chilichonse, tsono nadyako nyama ya nsembe yachiyanjano yopereka kwa Chauta, munthuyo achotsedwe pakati pa Aisraele anzake.” Chauta adauza Mose kuti, “Uza Aisraele kuti asadye mafuta ang'ombe, kapena ankhosa kapenanso ambuzi. Mafuta a nyama yofa yokha, ndi mafuta a nyama yojiwa ndi zilombo, angathe kuŵagwiritsa ntchito zina zilizonse, koma iwowo asadye. Pakuti munthu amene adya mafuta a nyama yoperekedwa kwa Chauta kuti ikhale nsembe yotentha pamoto, ayenera kuchotsedwa pakati pa Aisraele anzake. Ndiponso kulikonse kumene akakhale, asadye magazi aliwonse, ambalame kapena anyama. Munthu aliyense wophwanya lamulo limeneli, ayenera kuchotsedwa pakati pa Aisraele anzake.” Chauta adauza Mose kuti, “Uza Aisraele kuti, ‘Munthu amene apereka nsembe yake yachiyanjano kwa Chauta, abwere ndi gawo la nsembeyo kwa Chauta. Pa nsembe yake yachiyanjanoyo atengeko ndi manja ake zigawo zoyenera kuzitentha, zopereka kwa Chauta, ndiye kuti mafuta ndi nganga yomwe. Tsono ngangayo aiweyule kuti ikhale chopereka choweyula kwa ine. Apo wansembe atenthe mafuta pa guwa, koma ngangayo ikhale ya Aroni ndi ana ake. Wansembe mumpatsenso ntchafu ya ku dzanja lamanja, kuti ikhale chopereka cha pa nsembe yanu yachiyanjano. Pakati pa ana a Aroni, wansembe amene apereka magazi ndi mafuta a nsembe yachiyanjano, ndiye adzalandire ntchafu ya ku dzanja lamanja ngati chigawo chake. Choncho nganga yopereka moweyula manjayo, pamodzi ndi ntchafu yoperekayo, ndikuzichotsa zonsezo kwa Aisraele. Ndikuzichotsa pa nsembe zao zachiyanjano, ndipo ndikuzipereka kwa wansembeyo Aroni ndi kwa ana ake, kuti zikhale chigawo chao nthaŵi zonse. Chimenecho ndicho chigawo cha Aroni ndi cha ana ake, chotapa pa zopereka kwa Chauta zoyenera kutentha pa moto, chimene chidapatulidwa kuti chikhale chigawo chao, pa tsiku limene iwo adaperekedwa kuti akhale ansembe otumikira Chauta. Chauta ndiye amene adalamula Aisraele kuti azipereka zimenezi kwa ansembe, pa tsiku limene adadzozedwa. Zimenezo ndizo chigawo chao nthaŵi zonse pa mibadwo yao yonse.’ ” Ameneŵa ndiwo malamulo a nsembe zonsezi: yopsereza, ya chakudya, yopepesera machimo, yopepesera kupalamula, yakudzoza, ndiponso yachiyanjano. Malamulo ameneŵa ndi amene Chauta adapereka kwa Mose pa phiri lija la Sinai, pa tsiku limene adalamula Aisraele kuti abwere ndi nsembe zao kwa Chauta, ku chipululu cha Sinai chija. Chauta adauza Mose kuti, “Utenge Aroni ndi ana ake. Utengenso zovala, mafuta odzozera, ng'ombe yamphongo ya nsembe yopepesera machimo, nkhosa ziŵiri zamphongo, ndipo utengenso dengu la buledi wosafufumitsa. Tsono usonkhanitse mpingo wonse pa khomo la chihema chamsonkhano.” Mose adachitadi zomwe Chauta adamlamula. Choncho mpingo wonse udasonkhana pa khomo la chihema chamsonkhano. Ndipo adauza mpingo wonsewo kuti, “Nazi zimene Chauta walamula kuti zichitike.” Apo Mose adabwera ndi Aroni ndi ana ake, naŵasambitsa. Kenaka adamuveka mwinjiro Aroniyo, ndi kummanga lamba m'chiwuno. Adamuveka mkanjo ndi chovala cha efodi, ndipo adammanganso lamba wa efodiyo m'chiwuno. Tsono adamuveka chovala chapachifuwa, ndipo m'chovalacho adaikamo zinthu zotchedwa Urimu ndi Tumimu. Ndipo adamuveka nduŵira kumutu. Kumaso kwa nduŵirayo adaikako mphande yagolide, chizindikiro chopatulira, monga momwe Chauta adaalamulira Mose. Pambuyo pake Mose adatenga mafuta odzozera, nadzoza chihema chamsonkhano pamodzi ndi zonse zimene zinali m'menemo, ndipo adazipatula. Adawazako mafuta ena kasanu ndi kaŵiri pa guwa, nalidzoza guwalo pamodzi ndi zipangizo zake zonse. Adadzozanso mkhate pamodzi ndi phaka lake, kuti zikhale zopatulika. Mafuta ena odzozerawo adaŵathira pamutu pa Aroni, namdzoza, ndi kumsandutsa wopatulika. Kenaka adabwera ndi ana a Aroni aja naŵaveka miinjiro, naŵamanga malamba m'chiwuno, ndi kuŵaveka zikofiya kumutu. Pambuyo pake Mose adabwera ndi ng'ombe yamphongo ya nsembe yopepesera machimo, ndipo Aroni ndi ana ake adasanjika manja ao pamutu pa ng'ombe yamphongoyo. Kenaka Mose adaipha natenga magazi ake ndi kuŵapaka ndi chala chake pa nyanga za guwa molizungulira, ndipo adaliyeretsa. Adathiranso magazi patsinde pa guwalo nalipatula. Motero adachita mwambo wopepesera machimo. Tsono Mose adatenga mafuta onse akumatumbo ndi mphumphu ya mafuta akuchiŵindi, ndi imso ziŵiri pamodzi ndi mafuta ake omwe, ndipo adazitenthera paguwapo. Koma ng'ombe yamphongo ija, chikopa chake, nyama yake, ndi ndoŵe yake, zonsezi adazitenthera kunja kwa mahema, monga momwe Chauta adaalamulira Mose. Pambuyo pake adapereka nkhosa yamphongo ya nsembe yopsereza, ndipo Aroni ndi ana ake adasanjika manja ao pamutu pa nkhosayo. Kenaka Mose adaipha nathira magazi ake pa guwa mozungulira. Atadula nkhosayo nthulinthuli, Mose adatentha mutu wake ndi nthuli zija ndi mafuta ake omwe. Tsono atatsuka matumbo ake ndi miyendo yake, adazitenthanso. Motero adatentha nkhosa yathunthuyo pa guwa, kuti ikhale nsembe yopsereza, ya fungo lokoma, yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta, monga momwe Iye adaalamulira Mose. Tsono Mose adapereka nkhosa ina yamphongo, yoyenerera pa mwambo wodzoza ansembe. Ndipo Aroni pamodzi ndi ana ake adasanjika manja ao pamutu pa nkhosa yamphongoyo. Apo Mose adaipha, natengako magazi ake naŵapaka pa nsonga ya khutu la Aroni ku dzanja lamanja. Adapakanso pa chala chake chachikulu cha ku dzanja lamanja, ndi pa chala chake chachikulu cha ku phazi la dzanja lamanja. Pambuyo pake adabwera ndi ana a Aroni, ndipo Mose adapaka magazi pa nsonga za makutu ao a ku dzanja lamanja ndi pa zala zao zazikulu za ku dzanja lamanja, ndiponso pa zala zao zazikulu za ku phazi la ku dzanja lamanja. Kenaka Mose adathira magazi pa guwa molizungulira. Adatenga mafuta, mchira wamafuta, mafuta onse akumatumbo, mphumphu ya mafuta akuchiŵindi, imso ziŵiri ndi mafuta ake omwe, ndi ntchafu ya ku dzanja lamanja. Ndipo m'dengu la buledi wosafufumitsa, lopatulikira Chauta, adatengamo mtanda umodzi wa buledi wosafufumitsa, mtanda umodzi adatengamo mtanda umodzi wa buledi wosafufumitsa, mtanda umodzi wopaka mafuta ndi mtanda umodzi wa buledi wopyapyala. Zonsezo ataziika pa mafuta aja ndi pa ntchafu ya ku dzanja lamanja ija, adazikhazika m'manja mwa Aroni ndi m'manja mwa ana ake, ndipo adaziweyula kuti zikhale zopereka zoweyula kwa Chauta. Pambuyo pake Mose adazichotsa m'manja mwaomo nazitentha pa guwa, pamodzi ndi nsembe yopsereza ija, kuti zikhale nsembe yopereka pa mwambo wodzoza ansembe, ya fungo lokoma, nsembe yotentha pa moto yopereka kwa Chauta. Ndipo adatenga nganga naiweyula kuti ikhale chopereka choweyula pamaso pa Chauta. Chimenecho ndicho chigawo cha Mose cha nkhosa yamphongo yopereka pa mwambo wodzoza ansembe, potsata malamulo a Chauta kwa Mose. Tsono Mose adatengako mafuta odzozera aja ndi magazi amene anali pa guwa, nawaza Aroni ndi zovala zake ndiponso ana ake aja ndi zovala zao. Umu ndimo m'mene Mose adapatulira Aroni ndi zovala zake, ndiponso ana ake ndi zovala zao. Mose adauza Aroni ndi ana ake kuti, “Muphike nyamayo pa khomo la chihema chamsonkhano, ndipo muidyere pomwepo, pamodzi ndi buledi amene ali m'dengu la zopereka pa mwambo wodzoza ansembe, potsata zimene Chauta adaalamula kuti, ‘Aroni pamodzi ndi ake ndiwo adzadye zimenezo.’ Zotsala zake za nyamayo ndi za buledi zomwe, muzitenthe. Ndipo pa masiku asanu ndi aŵiri musatulukire kunja kwa chihema chamsonkhano, mpaka masiku a mwambo wodzoza ansembe atatha, poti mwambowu ndi wa masiku asanu ndi aŵiri. Chauta adatilamula kuti tikuchiteni zimene takuchitanizi, kuti ukhale mwambo wopepesera machimo anu. Muzikhala pa khomo la chihema chamsonkhano usiku ndi usana, masiku asanu ndi aŵiri, ndipo muzichita zimene Chauta wakulamulani, kuti mungafe. Zimenezi nzimene Chauta wandilamula.” Tsono Aroni ndi ana ake adachitadi zonsezo, monga momwe Chauta adaalamulira kudzera mwa Mose. Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, Mose adaitana Aroni, ana ake ndi atsogoleri a Aisraele. Adauza Aroniyo kuti, “Utenge mwanawang'ombe wamphongo kuti akhale nsembe yopepesera machimo, ndi nkhosa yamphongo kuti ikhale nsembe yopsereza. Zonsezo zikhale zopanda chilema, ndipo uzipereke pamaso pa Chauta. Tsono uuze Aisraele kuti, ‘Tengani tonde kuti muperekere nsembe yopepesera machimo. Mutengenso mwanawang'ombe ndi mwanawankhosa. Aŵiri onsewo akhale a chaka chimodzi, opanda chilema, kuti akhale nsembe yopsereza. Mutengenso ng'ombe ndi nkhosa kuti zikhale nsembe zachiyanjano zoti aziphere pamaso pa Chauta. Mubwerenso ndi zopereka za zakudya zosakaniza ndi mafuta, pakuti lero Chauta akuwonekerani.’ ” Zonse zimene Mose adalamula anthuwo, iwo adabwera nazo pakhomo pa chihema chamsonkhano. Ndipo mpingo wonse udasendera pafupi, nupembedza Chauta. Apo Mose adati, “Nazi zimene Chauta akukulamulani kuti muchite, kuti ulemerero wake ukuwonekereni.” Pamenepo Moseyo adauza Aroni kuti, “Sendera pafupi ndi guwa, ndipo upereke nsembe yopepesera machimo ndi nsembe yopsereza, kuti uchite mwambo wopepesera machimo ako ndi machimo a Aisraele. Ubwere ndi zopereka za anthuwo ndipo uchite mwambo wopepesera machimo ao, monga momwe Chauta walamulira.” Choncho Aroni adasendera pafupi ndi guwa, napha mwanawang'ombe woperekera nsembe yopepesera machimo, nsembeyo ya iye mwini wake. Ndipo ana ake adapereka magazi kwa Aroni. Iyeyo adaviika chala chake m'magazimo, naŵapaka pa nyanga za guwa, nathira magaziwo patsinde pa guwa lomwelo. Koma mafuta ndi imso, pamodzi ndi mphumphu ya mafuta akuchiŵindi, za nsembe yopepesera machimoyo, adazitenthera pa guwa, monga momwe Chauta adaalamulira Mose. Nyama yake ndi chikopa chake, adazitenthera kunja kwake kwa mahema. Tsono adapha nyama ya nsembe yopsereza, ndipo ana ake a Aroniyo atampatsira magazi, iye adawaza magaziwo pa guwa molizungulira. Pambuyo pake adampatsira nyama ya nsembe yopsereza yoduladula, pamodzi ndi mutu wake womwe, ndipo iye adazitentha pa guwa. Kenaka atatsuka matumbo ndi miyendo, adazitentha paguwa pomwepo, pamodzi ndi nsembe yopsereza ija. Tsono adapereka zopereka za anthuwo, natenga mbuzi ya nsembe yopepesera machimo a anthuwo, naipha nkuipereka ngati nsembe yopepesera machimo, monga adachitira ndi nsembe yopepesera machimo yoyambayo. Apo adabwera ndi nsembe yopsereza, naipereka potsata mwambo wake. Adaperekanso chopereka cha chakudya, natapako ufawo dzanja limodzi nautentha pa guwa, kuwonjezera pa nsembe yopsereza yam'maŵayo. Tsono adaphanso ng'ombe ndi nkhosa yamphongo, kuperekera anthu nsembe yachiyanjano. Pambuyo pake ana a Aroni adampatsira magazi, ndipo iye adathira magaziwo pa guwa molizungulira. Adampatsiranso mafuta ang'ombe ndi mafuta a nkhosa yamphongo, mchira wamafuta, mafuta okuta matumbo, imso pamodzi ndi mphumphu ya mafuta akuchiŵindi. Anawo adaika mafuta pa nganga, ndipo Aroni adatentha mafutawo pa guwa. Koma Aroni adaweyula ngangazo ndi ntchafu ya ku dzanja lamanja, kuti zikhale chopereka choweyula pamaso pa Chauta, monga momwe Mose adaalamulira. Tsono Aroni adakweza manja ake pa Aisraele naŵadalitsa. Ndipo adatsika paguwa, pomwe adaperekera nsembe yopepesera machimo, nsembe yopsereza ndi nsembe yachiyanjano. Pamenepo Mose pamodzi ndi Aroni adakaloŵa m'chihema chamsonkhano. Atatulukamo, adadalitsa anthu aja, ndipo ulemerero wa Chauta udaonekera anthu onsewo. Pompo moto udatuluka pamaso pa Chauta nupserezeratu nsembe yopsereza ndi mafuta omwe, zimene zinali paguwapo. Ndipo anthu ataona motowo, adafuula naŵeramitsa nkhope zao pansi. Ana a Aroni, Nadabu ndi Abihu, aliyense adatenga chofukizira lubani naikamo makala amoto. Pamakalapo adathirapo lubani, ndipo adapereka kwa Chauta moto umene Iye sadalamule. Tsono Chauta adatumiza moto nuŵapsereza, ndipo onsewo adafa pamaso pa Chauta. Apo Mose adauza Aroni kuti, “Pajatu Chauta adanena kuti, ‘Ndidzaonetsa ulemerero wanga kwa onse amene ali pafupi ndi Ine, ndipo ndidzalemekezedwa pamaso pa anthu onse.’ ” Koma Aroni adakhala chete osalankhula. Mose adaitana Misaele ndi Elizafani, ana a Uziyele, bambo wamng'ono wa Aroni, naŵauza kuti, “Senderani pafupi, achotseni abale anuŵa pa malo oyera ndipo muŵatulutsire kunja kwa mahema.” Iwo adasenderadi pafupi, naŵanyamula ali ndi mikanjo yao ndi kuŵatulutsira kunja kwa mahema, monga momwe Mose adaŵauzira. Tsono Mose adauza Aroni ndi ana ake Eleazara ndi Itamara kuti, “Musalilekerere tsitsi lanu, ndipo musang'ambe zovala zanu, kuti mungafe, ndiponso kuti mkwiyo ungagwere mpingo wonse. Koma abale anu a m'fuko lonse la Israele ndiwo alire chifukwa cha imfa ya moto umene Chauta watentha nawo anzanu. Musatulukire kunja kwa chihema chamsonkhano kuti mungafe, chifukwa mudadzozedwa ndi mafuta a Chauta.” Iwo adachita monga momwe Mose adanenera. Tsono Chauta adalankhula ndi Aroni namuuza kuti, “Usamwe vinyo kapena chakumwa china champhamvu, iwe ndi ana ako uli nawoŵa, pamene mukupita ku chihema chamsonkhano, kuwopa kuti mungafe. Limeneli likhale lamulo losatha pa mibadwo yanu yonse. Muzisiyanitsa pakati pa zinthu zoyera ndi zinthu wamba, ndiponso pakati pa zinthu zonyansa ndi zinthu zoyenera pa zachipembedzo. Muŵaphunzitse Aisraele malamulo onse amene Chauta adapereka kudzera mwa Mose.” Mose adauza Aroni ndi ana ake otsalira aja, Eleazara ndi Itamara, kuti, “Tengani zopereka za zakudya zimene zatsalako pa nsembe yotentha pa moto ija, yopereka kwa Chauta, ndipo muzidye zosafufumitsa pafupi pa guwa, pakuti zimenezi nzopatulika kopambana. Muzidye pa malo oyera, chifukwa zimenezi ndakugaŵiraniko kuchokera pa nsembe yotentha pa moto yopereka kwa Chauta, kuti zikhale zanu, iwe ndi ana ako. Ndithudi, zimenezi ndizo zimene Chauta adandilamula. Koma nganga yopereka moweyula manja ija, pamodzi ndi ntchafu yopereka, muzidyere pa malo aliwonse oyenera pa zachipembedzo, iweyo ndi ana ako aamuna ndi aakazi amene ali nawe. Zimenezi zapatsidwa kwa iwe kuti zikhale zako ndi za ana ako, kuchokera pa nsembe yachiyanjano imene aipereka Aisraele. Ntchafu yoperekayo ndi nganga yoweyulayo, abwere nazo pamodzi ndi zopereka za nsembe yamafuta yotentha pa moto, ndipo uziweyule, kuti zikhale chopereka choweyula pamaso pa Chauta. Zimenezi zikhale zako ndi za ana ako aamuna uli nawoŵa mpaka muyaya, monga momwe Chauta adaalamulira.” Tsono Mose adafunafuna mbuzi ya nsembe yopepesera machimo, ndipo adapeza kuti adaitentha kale. Ndipo adakalipira Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni otsala aja. Adati, “Chifukwa chiyani simudadyere pa malo oyera nsembe yopepesera machimo ija? Kodi si yopatulika kwambiri? Kodi siyoperekedwa kwa inu kuti muchotse machimo a mpingo wonse, kuti muŵachitire mwambo wopepesera machimo ao pamaso pa Chauta? Chifukwa magazi ake sadaloŵe nawo m'katikati mwa malo oyera kwambiri, mukadayenera kudyera zimenezi pa malo oyera, monga momwe ndidalamulira.” Ndipo Aroni adauza Mose kuti, “Taonani, lero anthu apereka nsembe yao yopepesera machimo ndi nsembe yao yopsereza pamaso pa Chauta. Komabe zinthu zoopsa zoterezi zandigwera ine. Nanga ndikadadya zopereka za nsembe yopepesera machimo lero, kodi Chauta akadakondwa?” Mose atamva zimenezo, adakhutira nazo. Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti, “Auzeni Aisraele kuti nyama zimene angathe kudya pakati pa nyama zonse za pa dziko lapansi ndi izi: ‘Nyama zonse zokhala ndi ziboda zogaŵikana, ndi zobzikula, angathe kudya zimenezo. Koma pakuti pa nyama zobzikula kapena za ziboda zogaŵikanazo, asadye izi: ngamira: imeneyi njonyansa kwa inu pa zachipembedzo, chifukwa ngakhale imabzikula, ziboda zake nzosagaŵikana. Mbira: imeneyi njonyansa kwa inu, chifukwa ngakhale imabzikula, ziboda zake nzosagaŵikana. Kalulu: ameneyu ndi wonyansa kwa inu, chifukwa ngakhale amabzikula, ziboda zake nzosagaŵikana. Nkhumba: imeneyi njonyansa kwa inu, chifukwa ngakhale ziboda zake nzogaŵikana ndipo mapazi ake ngogaŵikananso, koma siibzikula. Nyama ya zoŵeta zimenezo musamadye, ndipo zikafa musazikhudze. Zimenezi nzonyansa kwa inu.’ “Zamoyo zam'madzi zimene mutha kudya ndi izi: zonse zam'madzi zimene zili ndi zilimba ndi mamba, mungathe kudya, ngakhale zikhale zam'nyanja kapena zam'mitsinje. Koma zamoyo zonse zam'nyanja kapena zam'mitsinje zopanda zilimba ndi mamba, tizilombo tonse tam'madzi ndi zamoyo zonse zopezeka m'menemo, nzonyansa kwa inu. Zimenezo zikhale zonyansa kwa inu, ndipo musadye. Zikafa zikhalebe zonyansa kwa inu. Zamoyo zonse zam'madzi zopanda zilimba ndi mamba, nzonyansa kwa inu. “Ndipo mbalame zimene muyenera kuziyesa zonyansa, zoti simuyenera kudya, popeza kuti nzonyansa kwa inu, ndi izi: mphungu, nkhwazi, ndi muimba, nankapakapa, akamtema a mitundu yonse, akhungubwi a mitundu yonse nthiŵatiŵa, chipudo, kakoŵa, akabaŵi a mitundu yonse, kadzidzi, chiswankhono ndi mantchichi, tsekwe, vuwo, dembo, indwa, zimeza za mitundu yonse, nsadzu ndi mleme. “Zonse za miyendo inai, zouluka, nzonyansa kwa inu. Komabe pakati pa zouluka zonse za miyendo inai, mungathe kudya zokhazo zimene zili ndi miyendo yolumphira pa dothi. Pa zimenezo mungathe kudya izi: dzombe la mitundu yonse, atsokonombwe a mitundu yonse, nkhululu za mitundu yonse, ndi ziwala za mitundu yonse. Koma zamapiko zina zonse zokhala ndi miyendo inai nzonyansa kwa inu. “Tsono zimenezi mukazikhudza, zidzakuipitsani, ndipo aliyense wozikhudza zitafa, adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo. Aliyense akanyamula chiwalo chilichonse cha nyama zakufazo, achape zovala zake, komabe akhala woipitsidwa mpaka madzulo. Nyama iliyonse yokhala ndi ziboda zogaŵikana, koma mapazi ake osagaŵikana, kapenanso yosabzikula, njonyansa imeneyo kwa inu, ndipo aliyense woikhudza, adzakhala woipitsidwa. Pakati pa nyama zonse za miyendo inai, nyama zonse zokhala ndi zikhadabo ku mapazi, nzonyansa kwa inu, ndipo aliyense wozikhudza zitafa, adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo. Ndipo munthu amene anyamula nyamazi zitafa, achape zovala zake, komabe akhala woipitsidwa mpaka madzulo. Zimenezi nzonyansa kwa inu. “Tsono zokwaŵa zonse zimene zili zonyansa kwa inu ndi izi: likongwe, mbeŵa, ng'azi za mitundu yonse, gondwa, mng'anzi, buluzi dududu ndi birimankhwe. Zimenezi nzonyansa kwa inu pakati pa zokwaŵa zonse. Munthu aliyense wozikhudza zitafa, adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo. Ndipo nyama zimenezi zikagwera pa chinthu chilichonse zitafa, chinthucho chidzakhala chonyansa, chingakhale chamtengo, kapena chovala, kapena chikopa, kapena chiguduli, kapena chipangizo chilichonse chogwiritsa ntchito iliyonse. Chinthucho achiviike m'madzi, koma chidzakhalabe chonyansa mpaka madzulo. Pambuyo pake chidzakhala chabwino. Tsono china chilichonse mwa zimenezi chikagwera m'mbiya yadothi, zonse za m'menemozo zidzakhala zonyansa, ndipo mbiyayo muiphwanye. Madzi am'mbiyamo akathira pa chakudya chilichonse, chakudyacho chidzakhala chonyansa. Chakumwa chilichonse cha m'mbiya ya mtundu umenewo chidzakhala chonyansa. Chiwalo chilichonse cha nyama yakufa chikagwera pa chinthu chilichonse, chinthucho chidzakhala chonyansa, kaya ndi uvuni kapena chitofu, zonsezo aziphwanye, poti nzonyansa zimenezo, ndipo zidzakhala zonyansa kwa inu. Koma kasupe kapena chitsime chamadzi zidzakhalabe zabwino, ngakhale kuti chilichonse chokhudza nyama chidzakhala chonyansa. Chiwalo chilichonse cha nyama zakufazo chikagwera pa mbeu zimene anthu akuti abzale, mbeu zimenezo zikhalabe zabwino. Koma mbeuzo zikakhala zonyowa ndi madzi, ndipo chiwalo chilichonse cha nyama zakufa chigwera pa mbeuzo, zidzakhala zonyansa kwa inu. “Munthu akakhudza nyama yofa yokha imene anthu amadya, munthuyo adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo. Ndipo munthu amene adyako nyamayo, achape zovala zake, komabe adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo. Nayenso amene anyamula nyama yakufayo, achape zovala zake, komabe adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo. “Chinthu chilichonse chokwaŵa pansi nchonyansa, ndipo musadye. Chinthu chilichonse chokwaŵa ndi kumimba, ndiponso chilichonse cha miyendo inai kapena cha miyendo yambirimbiri, kungoti zonse zokwaŵa pansi, musadye poti nzonyansa kwa inu. Musadzisandutse oipitsidwa ndi chokwaŵa chilichonse, musadziipitse nazo, kuti mungasanduke oipitsidwa. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu. Tsono mudziyeretse, ndipo mukhale oyera pakuti Ine ndine woyera. Musadziipitse ndi chinthu chokwaŵa pansi chilichonse. Pakuti Ine ndine Chauta, amene ndidakutulutsani ku dziko la Ejipito kuti ndikhale Mulungu wanu. Tsono mukhale oyera, pakuti Ine ndine woyera.” Limeneli ndilo lamulo lonena za nyama, mbalame, chamoyo chilichonse choyenda m'madzi, ndi chinthu chilichonse chokwaŵa pansi, kuti muzisiyanitsa pakati pa zonyansa ndi zosanyansa, ndiponso pakati pa zamoyo zimene mungathe kudya ndi zimene simuyenera kudya. Chauta adauza Mose kuti, “Uza Aisraele kuti mkazi akakhala ndi pakati, nabala mwana wamwamuna, adzakhala woipitsidwa masiku asanu ndi aŵiri, monga pa nthaŵi yake yakusamba. Ndipo pa tsiku lachisanu ndi chitatu mwanayo aumbalidwe. Mkaziyo adikirebe masiku ena 33, kuti ayeretsedwe ku matenda ake. Asakhudze kanthu kopatulika kalikonse, ndipo asaloŵe m'malo oyera, mpaka masiku akudziyeretsa atatha. Koma akabala mwana wamkazi, adzakhala woipitsidwa masabata aŵiri monga pa nthaŵi yake yakusamba. Ndipo mkaziyo adikirebe masiku ena 66, kuti ayeretsedwe ku matenda ake. “Tsono masiku akudziyeretsa kwake aja atatha, kapena ndi a mwana wamwamuna kapena a mwana wamkazi, abwere kwa wansembe ndi mwanawankhosa wa chaka chimodzi pa khomo la chihema chamsonkhano, kuti nkhosayo ikhale nsembe yopsereza. Abwerenso ndi bunda la nkhunda kapena njiŵa, kuti aperekere nsembe yopepesera machimo. Wansembeyo apereke zimenezo pamaso pa Chauta potsata mwambo wopepesera mkaziyo. Apo mkaziyo adzakhala woyeretsedwa ku matenda ake. Limeneli ndi lamulo la mkazi amene abala mwana wamwamuna kapena wamkazi. Koma ngati alibe mwanawankhosa, atenge njiŵa ziŵiri kapena maundaankhunda aŵiri, imodzi ikhale ya nsembe yopsereza, ndipo inayo ikhale ya nsembe yopepesera machimo. Tsono wansembe achite mwambo wopepesera, ndipo mkaziyo adzakhala woyeretsedwa.” Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti, “Munthu akakhala ndi chithupsa pathupi pake, kapena m'buko, kapena chikanga, ndipo mwina nkusanduka ngati nthenda ya khate pakhungu pakepo, munthuyo abwere naye kwa wansembe Aroni kapena kwa aliyense mwa ana ake amene ali ansembe. Wansembe aonetsetse pakhungu pali nthendapo. Akapeza kuti ubweya wa pamalo pali nthendapo wasanduka woyera, ndipo kuti nthendayo yazama ndithu kupitirira khungu, ndiye kuti limenelo ndi khate. Wansembe atamuwonetsetsa ndithu, amutchule kuti ndi woipitsidwa. Koma pakhungupo pakamaoneka kuti mpoyera, ndipo nthendayo sidapitirire khungu, ndipo ubweya wapamalopo sudasanduke woyera, wansembeyo amuike padera munthu wodwalayo masiku asanu ndi aŵiri. Wansembe amuwonetsetse wodwalayo pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri. Akaiwona nthendayo kuti sidafalikire pa khungu, pamenepo wansembeyo amtsekere munthu uja masiku asanu ndi aŵiri ena. Tsono wansembe uja amuwonetsetsenso wodwalayo pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri. Pakhungu pakakhala pothimbirira, nthendayo yosafalikira pakhungupo, wansembe amutchule munthuyo kuti ndi wosaipitsidwa. Umenewo ndi m'buko chabe, tsono wodwalayo achape zovala zake, ndipo adzakhala woyeretsedwa. Koma m'bukowo ukafalikira pa khungu, munthuyo atadziwonetsa kale kwa wansembe kuti amuyeretse, munthuyo akaonekerenso pamaso pa wansembe. Wansembe amuwonetsetsenso munthuyo. Akaona kuti m'bukowo wafalikiradi pa khungu, atchule wodwalayo kuti ndi woipitsidwa, limenelo ndi khate. “Munthu akagwidwa ndi nthenda ya khate, abwere naye kwa wansembe. Wansembe amuwonetsetse. Akakhala ndi chithupsa cha maonekedwe oyera pa khungu, chimene chasandutsa ubweya wapamalopo kukhala woyera, ndipo pachithupsapo pakakhala zilonda, limenelo ndi khate lachikhalire limene lili pakhungu pakelo, ndipo wansembe amutchule kuti ndi woipitsidwa. Sikufunika kumtsekera chifukwa ndi woipitsidwadi. Khatelo likafalikira pa khungu, kotero kuti likhala litagwira khungu lonse la munthu wodwalayo kuyambira kumutu mpaka kumapazi, monga m'mene wansembe angaonere, pamenepo wansembeyo aonetsetse. Khatelo likakhala litagwira thupi lonse, wodwalayo amutchule kuti ndi wosaipitsidwa. Thupi lonse lasanduka loyera ndipo munthuyo ndi wosaipitsidwa. Koma pathupi pake pakaoneka zilonda, ndiye kuti munthuyo ndi woipitsidwa. Tsono wansembe aonetsetse zilondazo, ndipo munthu wodwalayo amtchule kuti ndi woipitsidwa. Zilondazo nzoipitsa poti limenelo ndi khate. Koma zilondazo zikasinthikanso ndi kusanduka zoyera, pamenepo munthu wodwalayo abwere kwa wansembe. Tsono wansembeyo amuwonetsetse. Zilondazo zikakhala kuti zasanduka zoyera, wansembeyo amutchule munthu wodwalayo kuti ndi wosaipitsidwa. Ndi woyera ameneyo. “Pa khungu la munthu wodwalayo pakakhala chithupsa choti chidapola, ndipo pamene panali chithupsacho pakatuluka zotupatupa zoyera kapena banga loyera mofiirira, aziwonetse kwa wansembe. Wansembe aonetsetse bwino, ndipo chithupsacho chikazama, ubweya wake nusanduka woyera, wansembeyo amutchule munthu wodwala uja kuti ndi woipitsidwa. Imeneyo ndi nthenda ya khate imene yaphulika pachithupsapo. Koma wansembe akaonetsetsa, napeza kuti ubweya wake sudasanduke woyera, ndipo chithupsacho sichidazame, koma chikuzimirira, wansembeyo amuike padera wodwalayo masiku asanu ndi aŵiri. Nthendayo ikafalikira pa khungu, wansembe amutchule wodwalayo kuti ndi woipitsidwa, limenelo ndi khate. Koma bangalo likakhala pa malo amodzi, osafalikira, chimenecho nchipsera cha chithupsa. Wansembe amutchule wodwalayo kuti ndi wosaipitsidwa. “Munthu akakhala ndi bala lamoto, ndipo chilonda cha balalo chikasanduka banga loyera mofiirira kapena loyera kumene, wansembe aliwonetsetse. Ubweya wapabangapo ukasanduka woyera, ndipo balalo likaoneka kuti lazama, limenelo ndi khate lomwe laphulika pa balalo. Wansembe atchule wodwalayo kuti ndi woipitsidwa. Imeneyo ndi nthenda ya khate. Koma wansembe akaonetsetsa, napeza kuti ubweya wake sudasanduke woyera, ndipo balalo silidazame, koma likuzimirira, wansembe amuike padera wodwalayo masiku asanu ndi aŵiri. Pa tsiku lachisanu ndi chiŵirilo, ngati bangalo lafalikira pa khungu, wansembe amutchule wodwalayo kuti ndi woipitsidwa. Imeneyo ndi nthenda ya khate. Koma bangalo likakhala pa malo amodzi losafalikira pa khungu, ndipo likuzimirira, limenelo ndi thuza la balalo. Wansembeyo amtchule wodwalayo kuti ndi wosaipitsidwa, popeza kuti nchipsera cha bala lamoto chabe. “Mwamuna kapena mkazi akakhala ndi nthenda kumutu kapena kundevu, wansembe aiwonetsetse nthendayo. Ikaoneka kuti ikuzama, ndipo ubweya ukakhala wachikasu ndi wotetemera, wansembeyo amutchule wodwalayo kuti ndi woipitsidwa. Imeneyo ndi mfundu yonyerenyesa, khate lakumutu kapenanso lakundevu. Wansembe ataiwonetsetsa mfundu yonyerenyesayo, niwoneka kuti sidazame, ndipo palibe ubweya wakuda pamalopo, wansembeyo amuike padera munthu wodwala mfundu yonyerenyesayo masiku asanu ndi aŵiri. Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, wansembe aiwonenso nthendayo. Mfunduyo ikakhala yakuti sidafalikire, ndipo palibe ubweya wachikasu, ndipo mfunduyo ikaoneka kuti sidazame, wodwalayo amete, koma mfunduyo asaimete. Wansembe amtsekere masiku asanu ndi aŵiri ena munthu wodwala mfundu yonyerenyesayo. Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, wansembe aiwonetsetsenso mfunduyo, ndipo ikakhala yakuti sidafalikire pa khungu, ndiponso ikaoneka kuti sidazame, wansembe atchule wodwalayo kuti ndi wosaipitsidwa. Tsono wadwalayo achape zovala zake, ndipo akhale wosaipitsidwa. Koma mfunduyo ikafalikira pa khungu, wodwalayo atayeretsedwa kale, pamenepo wansembe amuwonetsetse wodwalayo. Mfunduyo ikakhala itafalikira pa khungu, wansembe asafunefune ubweya wachikasu ai, munthuyo ndi woipitsidwa. Koma wansembe akaipenyetsetsa mfunduyo napeza kuti pamera ubweya wakuda, ndiye kuti mfunduyo ndi yopola. Tsono wansembe amtchule wodwalayo kuti ndi wosaipitsidwa. “Mwamuna kapena mkazi akakhala ndi maŵanga oyera pa khungu, wansembe aonetsetse bwino. Maŵanga apakhunguwo akakhala oyerera, ndiye kuti ndi mibuko chabe yotuluka pakhungupo. Tsono munthuyo ndi wosaipitsidwa. “Tsitsi la munthu likatha kumutu chapankhongo, ndiye kuti ndi dazi limenelo, koma munthuyo ndi wosaipitsidwa. Munthu akakhala wopanda tsitsi pa mphumi ndiponso m'litsipa, ndiye kuti ali ndi dazi lapamphumi, koma ndi wosaipitsidwa. Koma pa dazi lapankhongo kapena lapamphumi pakakhala banga la nthenda loyera mofiirira, limenelo ndi khate limene likutuluka pa nkhongo kapena pa mphumi. Tsono wansembe amuwonetsetse wodwalayo, ndipo banga lotupalo likakhala loyera mofiirira pa dazi lapankhongolo kapena lapamphumilo, monga m'mene limaonekera khate pa khungu, ndiye kuti munthuyo ndi woipitsidwa ndithu. Wansembe ayenera kumtchula kuti ndi woipitsidwa, ali ndi khate lakumutu. “Munthu wakhate avale nsanza, ndipo tsitsi lake alilekerere, aphimbe mlomo wake wam'mwamba, ndipo azifuula kuti, ‘Ndine woipitsidwa, ndine woipitsidwa.’ Wodwalayo adzakhalabe woipitsidwa nthaŵi zonse pamene ali ndi nthendayo, ndipo akhale payekha kunja kwa mahema. “Chovala chaubweya kapena chathonje chikakhala ndi nguwi kapena nsalu yathonje kapena yaubweya, kapenanso chikopa kapena chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, ndipo nguwiyo ikakhala ndi maonekedwe achisipu kapena ofiira pa chovalapo, kapena pa thonje loluka, kapena pa chikopa, kaya pa chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, imeneyo ndi nguwi ndithu, ndipo chovalacho achiwonetse kwa wansembe. Wansembeyo aiwonetsetse nguwiyo. Chovalacho achiike padera masiku asanu ndi aŵiri. Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri aiwonetsetsenso nguwiyo. Ikakhala itafalikira pa chovalacho, kapena pa chikopa cha ntchito ya mtundu uliwonse, imeneyo ndi nguwi yoopsa. Chovalacho ndi choipitsidwa. Tsono wansembe achitenthe chovalacho, chifukwa nguwiyo yaipitsa chovala chaubweya kapena chathonjecho, kapena chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, poti imeneyo ndi nguwi yoopsa. Chinthucho achitenthe. “Wansembe akaonetsetsa napeza kuti nguwiyo sidafalikire pa chovalacho, kapena pa chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, wansembeyo alamule kuti achape chovalacho, ndipo achiike padera masiku asanu ndi aŵiri ena. Ndipo wansembe achiwonetsetse chovala chimenecho chitachapidwa. Ngati banga la nguwiyo silidasinthe maonekedwe ake, ngakhale kuti siidafalikire, chovalacho nchoipitsidwa ndithu. Muchitenthe, osasamala zakuti banga la nguwiyo lili kumbuyo kapena kumaso. “Koma wansembe akaonetsetsa napeza kuti nguwiyo njothimbirira atachapa chovalacho, ang'ambe banga la nguwilo pa chovala chathonjecho kapena chachikopacho. Bangalo likaonekanso pa chovalacho kapena pa chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, ndiye kuti nguwiyo ikufalikira. Zonse zanguwizo muzitenthe. Koma chovala, kapena chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, mukachapa, tsono nguwiyo nkuchoka, muchapenso kachiŵiri, ndipo chidzakhala choyeretsedwa.” Limeneli ndi lamulo la nguwi yokhala pa chovala chaubweya kapena m'chovala chathonje, kapenanso m'chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa, kuti muzisiyanitsa pakati pa chinthu choipitsidwa ndi chosaipitsidwa. Chauta adauza Mose kuti, “Lamulo la munthu wakhate pa tsiku la kuyeretsedwa kwake nali: Abwere naye kwa wansembe. Tsono wansembeyo atuluke kunja kwa mahema, ndipo amuwonetsetse wodwalayo. Ngati wakhateyo apezeke kuti wachira, wansembe alamule anthu kuti wodwala amene akuti ayeretsedweyo, amtengere mbalame zamoyo ziŵiri zimene Ayuda amaloledwa kudya, nthambi yamkungudza, kansalu kamlangali ndi kanthambi ka hisope. Wansembeyo alamule anthuwo kuti mbalame imodzi aiphere m'mbale yadothi pamwamba pa madzi atsopano. Wansembe atenge mbalame yamoyo ija pamodzi ndi nthambi yamkungudza ija, kansalu kamlangali kaja ndi kachitsamba ka hisope kaja. Zonsezo pamodzi ndi mbalame yamoyoyo, aziviike m'magazi a mbalame yomwe adaiphera m'mbale pamwamba pa madzi atsopano ija. Tsono wansembe awaze magazi kasanu ndi kaŵiri pa munthu amene akuti amuyeretse khateyo. Pamenepo wodwalayo amutche kuti ndi woyeretsedwa, ndipo aiwulutsire ku thengo mbalame yamoyoyo. Wodwala amene wayeretsedwayo, achape zovala zake, amete tsitsi lake lonse, ndipo asambe m'madzi; tsono atatero, adzakhala woyeretsedwa. Atatha zonsezo aloŵe chakumahema, koma akhale kunja kwa hema lake masiku asanu ndi aŵiri. Pa tsiku lotsiriza amete tsitsi lake lonse kumutu. Ametenso ndevu zake pamodzi ndi nsidze zomwe, tsitsi lake lonse ndithu. Kenaka achape zovala zake ndi kusamba, ndipo atatero, adzakhala woyeretsedwa. “Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, wodwalayo atenge anaankhosa amphongo aŵiri opanda chilema, atengenso mwanawankhosa mmodzi wamkazi, wa chaka chimodzi, wopanda chilema, ndi chochepereka cha chakudya wosalala wolemera makilogaramu atatu, wosakaniza ndi mafuta, ndiponso mafuta okwanira limodzi mwa magawo atatu a lita. Wansembe amene ayeretse wodwalayo, aimiritse munthu woti ayeretsedweyo ali ndi zopereka zake zonse, pamaso pa Chauta, pakhomo pa chihema chamsonkhano. Wansembe atengeko mwanawankhosa wamphongo mmodzi ndi kumpereka kuti akhale nsembe yopepesera kupalamula, pamodzi ndi mafuta aja. Aziweyule, kuti zikhale zopereka zoweyula pamaso pa Chauta. Mwanawankhosayo amuphere pamalo pomwe amaphera nyama yoperekera nsembe yopepesera machimo ndi nsembe yopsereza, ndiye kuti pa malo oyera aja, pakuti chopereka chopepesera kupalamula ndi chake cha wansembe, monga momwe chimakhalira chopereka chopepesera machimo. Zoperekazo nzoyera kopambana. Wansembe atengeko magazi a nyama yoperekera nsembe yopepesera kupalamula, ndi kuŵapaka pa nsonga ya khutu la ku dzanja lamanja la munthu woti ayeretsedweyo. Apakenso pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja, ndi pa chala chachikulu cha ku phazi la ku dzanja lamanja. Wansembe atapeko mafuta pang'ono, nkuŵathira m'dzanja lake lakumanzere. Ndipo aviike chala chake cha ku dzanja lamanja m'mafuta amene ali m'dzanja lakumanzerewo, ndi kuwazako mafutawo ndi chala chake kasanu ndi kaŵiri pamaso pa Chauta. Mafuta otsala m'dzanja la wansembeyo, aŵapakeko pa nsonga ya khutu la ku dzanja lamanja la munthu woyeretsedwa uja, ndiponso pa chala chake chachikulu cha ku dzanja lamanja. Aŵapakenso pa chala chachikulu cha ku phazi la ku dzanja lamanja, pamalo pamene anali atapaka magazi aja a nyama yoperekera nsembe yopepesera kupalamula ija. Mafuta otsala m'dzanja la wansembe, aŵathire pamutu pa munthu woti ayeretsedwe uja. Ndimo m'mene wansembe amchitire munthuyo mwambo wompepesera pamaso pa Chauta. Pambuyo pake wansembe apereke nsembe yopepesera machimo, kuti achite mwambo wompepesera munthu woti ayeretsedwe khate lake uja. Kenaka wansembeyo aphe nyama yoperekera nsembe yopsereza, ndipo aipereke pamodzi ndi chopereka cha chakudya pa guwa. Atatero ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera machimo a munthu wodwalayo, ndipo pamenepo munthuyo adzakhala woyeretsedwa. “Koma munthu wodwalayo akakhala wosauka, kuti alibe zonsezo, apereke mwanawankhosa wamphongo kuti akhale nsembe yopepesera kupalamula. Aipereke moweyula manja, kuti achite mwambo wompepesera. Aperekenso kilogaramu limodzi la ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, kuti ukhale nsembe yaufa, pamodzi ndi mafuta okwanira limodzi mwa magawo atatu a lita. Aperekenso njiŵa ziŵiri kapena maundaankhunda aŵiri, monga m'mene angathere. Imodzi ikhale ya nsembe yopepesera machimo, inayo ikhale ya nsembe yopsereza. Pa tsiku lachisanu ndi chitatu zonsezo abwere nazo kwa wansembe, pakhomo pa chihema chamsonkhano pamaso pa Chauta, kuti munthuyo ayeretsedwe. Wansembe atenge mwanawankhosa woperekera nsembe yopepesera kupalamula, pamodzi ndi mafuta aja, ndipo aziweyule, kuti zikhale zopereka zoweyula pamaso pa Chauta. Tsono nkhosa yoperekera nsembe yopepesera kupalamulayo aiphe. Atengeko magazi ake ndi kuŵapaka pa nsonga ya khutu la ku dzanja lamanja la munthu amene ayeretsedweyo, ndi pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja, pamodzi ndi pa chala chachikulu cha ku phazi la ku dzanja lamanja. Kenaka wansembe athireko mafuta m'dzanja lake lamanzere, awazeko mafutawo kasanu ndi kaŵiri ndi chala cha ku dzanja lamanja pamaso pa Chauta. Apakekonso mafuta omwewo pa nsonga ya khutu la ku dzanja lamanja la munthu amene ayeretsedweyo. Aŵapakenso pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja pamodzi ndi pa chala chachikulu cha ku phazi la ku dzanja lamanja, pamalo pomwe anali atapaka magazi a nyama yoperekera nsembe yopepesera kupalamula ija. Mafuta otsala amene ali m'dzanja la wansembe aŵapake pamutu pa munthu amene ayeretsedweyo, kuti amchitire mwambo wopepesera machimo pamaso pa Chauta. Tsono malinga ndi m'mene adapezeramo, apereke njiŵa ziŵiri kapena maundaankhunda aŵiri. Azipereke ziŵirizo kuti imodzi ikhale nsembe yopepesera machimo, ndipo ina ikhale nsembe yopsereza, pamodzi ndi chopereka cha chakudya. Atatero, ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera machimo a munthu amene ayeretsedweyo pamaso pa Chauta. Limeneli ndilo lamulo la munthu wakhate amene alibe zinthu zoperekera kuyeretsedwa kwake.” Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti “Mukakaloŵa m'dziko la Kanani limene ndikukupatsani kuti likhale lanu, ndipo ndikakagwetsa ndere m'nyumba iliyonse m'dziko lanulo, mwiniwake nyumbayo adzapite kwa wansembe, akamuuze kuti, ‘Ndikuwona ngati kuti m'nyumba mwanga muli ndere.’ Tsono wansembe asanawonetsetse nderezo, alamule kuti anthu atulutse zinthu zonse m'nyumbamo, kuti zam'nyumbazo angazitchule kuti nzoipitsidwa. Pambuyo pake wansembeyo aloŵe m'nyumbamo kuti aonemo. Ndipo aonetsetse nderezo. Akapezeka kuti zili m'khoma la nyumba, niziwoneka ndi maanga achisipu kapena ofiira, ndipo ikaoneka kuti yaloŵera mpaka m'kati, wansembeyo atuluke m'nyumbamo ndi kupita pa khomo, ndipo aitseke nyumbayo masiku asanu ndi aŵiri. Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri wansembeyo abwerenso kudzayang'ana. Nderezo zikakhala kuti zafalikira m'makoma a nyumbayo, wansembeyo alamule kuti anthu agamule miyala m'mene muli nderezo, ndipo akaitaye ku dzala kunja kwa mzinda. Pambuyo pake wansembe auze anthu kuti apale makoma onse m'kati mwa nyumbayo, ndipo dothi akupalalo akalitaye ku dzala kunja kwa mzinda. Tsono anthuwo atenge miyala ina ndi kuiloŵetsa m'malo mwa miyala adagumula ija, mwiniwakeyo atengenso dothi lina ndipo amate nyumbayo. “Nderez zikabukanso m'nyumba atagumula kale miyala ija, ndipo ataipala ndi kuimatanso, wansembe apite kukayang'ana. Zikakhala kuti zafalikiranso m'nyumbamo, ndiye kuti ndere zomwe zidafalikira m'nyumbamo ndi zoopsa. Nyumbayo njoipitsidwa. Aigwetse nyumbayo, tsono miyala yake, mitengo yake pamodzi ndi dothi limene adamatira nyumbayo, zonse akazitaye ku dzala kunja kwa mzinda. Ndipo munthu amene waloŵa m'nyumbamo itatsekedwa, adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo. Munthu amene wagona m'nyumbamo achape zovala zake, ndipo amene wadyeramo nayenso achape zovala zake. “Koma wansembe akabwera naonetsetsa m'nyumbamo ndi kupeza kuti nthendayo sidafalikiremo, nyumbayo ataimata kale, wansembe aitchule nyumbayo kuti njosaipitsidwa, poti nderezo mulibe. Mwiniwake wa nyumbayo atenge timbalame tiŵiri, nthambi yamkungudza, kansalu kamlangali, ndi kachitsamba ka hisope, kuti zikhale zoyeretsera nyumbayo. Kamodzi mwa timbalame tiŵirito, wansembe akaphere m'mbale yadothi pamwamba pa kasupe. Kenaka atenge nthambi yamkungudza, kachitsamba ka hisope, ndi kansalu kamlangali, pamodzi ndi kambalame kamoyo kaja, zonsezo aziviike m'magazi a kambalame kophedwa kaja, ndiponso m'madzi atsopano aja, ndipo awaze nyumbayo kasanu ndi kaŵiri. Atatero, ndiye kuti wansembeyo waiyeretsa nyumbayo ndi magazi a mbalame, madzi atsopano, mbalame yamoyo, nthambi yamkungudza, kachitsamba ka hisope, ndiponso kansalu kamlangali. Mbalame yamoyo ija aiwulutsire kunja kwa mzinda ku thengo. Pamenepo ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera nyumbayo, ndipo idzakhala yoyeretsedwa.” Izi ndizo zimene muyenera kuchita ngati muona kuti mwadetsedwa chifukwa cha khate la mfundu yonyerenyesa, nguwi la pa chovala, ndere za m'nyumba, khate lachithupsa, khate lam'buko ndi khate labanga. Malamulo ameneŵa ngonena za chinthu choipitsidwa ndi chosaipitsidwa. Atsatidwe pa nthenda zonse za khate. Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti, “Muuze Aisraele kuti: Mwamuna aliyense akakhala ndi nthenda yotulutsa mafinya ku maliseche ake, zimenezo nzonyansa ndithu. Lamulo lake lokhudza za kudziipitsa ndi zonyansa zotuluka ku maliseche a munthu nali: malisechewo akamatulutsabe mafinya, kaya aleka, munthuyo ndi woipitsidwa ndithu. Bedi lililonse limene munthu wotulutsa mafinyayo agonepo, lidzakhala loipitsidwa. Chinthu chilichonse chimene akhalepo, chidzakhala choipitsidwa. Aliyense wokhudza bedi lake achape zovala zake, ndipo asambe, koma akhalabe woipitsidwa mpaka madzulo. Munthu amene akhale pa chinthu chilichonse chimene wotulutsa mafinyayo adakhalapo, achape zovala zake, ndipo asambe thupi lonse, koma akhalabe woipitsidwa mpaka madzulo. Aliyense wokhudza thupi la munthu wotulutsa mafinyayo, achape zovala zake ndipo asambe, koma akhalabe woipitsidwa mpaka madzulo. Munthu wotulutsa mafinya akalavulira malovu mnzake amene ali wosaipitsidwa, mnzakeyo achape zovala zake ndipo asambe thupi lonse, koma akhalabe woipitsidwa mpaka madzulo. Ndipo chokhalira chilichonse chapakavalo, chimene munthu wotulutsa mafinya uja adakhalapo, chidzakhala choipitsidwa. Aliyense amene akhudze chinthu chilichonse chimene munthuyo adakhalapo, adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo. Aliyense amene achinyamule, achape zovala zake, ndipo asambe thupi lonse, koma akhalabe woipitsidwa mpaka madzulo. Aliyense amene munthu wotulutsa mafinyayo amkhudze asanasambe m'manja, achape zovala zake, ndipo asambe thupi lonse, koma akhalabe woipitsidwa mpaka madzulo. Chiŵiya chadothi chimene munthu wotulutsa mafinyayo akhudze, achiphwanye, ndipo chiŵiya chilichonse chamtengo achitsuke m'madzi. “Munthu wotulutsa mafinyayo akaona kuti wachira, aŵerenge masiku asanu ndi aŵiri a kuyeretsedwa kwake, kenaka achape zovala zake, asambe pa kasupe, ndipo adzakhala woyeretsedwa. Pa tsiku la chisanu ndi chitatu atenge njiŵa ziŵiri kapena maundaankhunda aŵiri, ndi kubwera nazo pamaso pa Chauta pakhomo pa chihema chamsonkhano, ndipo azipereke kwa wansembe. Wansembeyo apereke zimenezo, kuti imodzi ikhale nsembe yopepesera machimo, ina ikhale nsembe yopsereza. Pamenepo wansembeyo ndiye kuti wachita mwambo wopepesera pamaso pa Chauta machimo a munthu wotulutsa mafinya uja. “Mwamuna akataya pansi mbeu yake yaumuna, asambe thupi lake lonse koma akhalabe woipitsidwa mpaka madzulo. Chovala chilichonse ndi chikopa chilichonse pomwe pagwera mbeu yaumunapo achitsuke, koma zikhalabe zoipitsidwa mpaka madzulo. Mwamuna akataya mbeu yake pogona ndi mkazi, onse aŵiriwo asambe, koma akhalabe oipitsidwa mpaka madzulo. “Mkazi akakhala wosamba, ndipo ikakhala nthaŵi yeniyeni yakusamba, akhala woipitsidwa masiku asanu ndi aŵiri, aliyense amene amkhudze akhala woipitsidwa mpaka madzulo. Ndipo chilichonse chimene mkaziyo agonere ali woipitsidwabe, chikhala choipitsidwa. Chinthu china chilichonse chimene akhalire chikhala choipitsidwa. Aliyense wokhudza bedi la mkaziyo achape zovala zake, ndipo asambe thupi lonse, koma akhala woipitsidwa mpaka madzulo. Aliyense wokhudza chimene mkaziyo amakhalapo, achape zovala zake ndipo asambe thupi lonse, koma akhalabe woipitsidwa mpaka madzulo. Kaya chinthucho chikhale bedi kapena chinthu china chilichonse chimene mkaziyo amakhalapo, munthu akachikhudza, akhala woipitsidwa mpaka madzulo. Mwamuna aliyense akagona ndi mkazi amene akusambabe, mwamunayo akhala woipitsidwa masiku asanu ndi aŵiri. Ndipo bedi lililonse limene mwamunayo agonepo likhala loipitsidwa. “Mkazi akataya magazi masiku ambiri osakhala nthaŵi yake yosamba, kapena akamasambabe kupitirira pa nthaŵi yake ya kusamba, masiku onsewo mkaziyo ali wotaya magazi ndi woipitsidwa, monga momwe amakhalira pa masiku ake osamba. Bedi lililonse limene mkaziyo agonepo pa masiku onse pamene ali wotaya magazi, lidzakhala loipitsidwa. Ndipo zonse zimene amakhalirapo zikhala zoipitsidwa, monga momwe zimakhalira zoipitsidwa pamene ali wosamba pa nthaŵi yake. Aliyense wokhudza zimenezi akhala woipitsidwa. Tsono achape zovala zake ndi kusamba thupi lonse, koma akhala woipitsidwabe mpaka madzulo. Atatha matenda a kusamba kwakeko, mkazi aŵerenge masiku asanu ndi aŵiri, ndipo pambuyo pake akhala woyeretsedwa. Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, mkaziyo atenge njiŵa ziŵiri kapena maundaankhunda aŵiri, ndipo abwere nazo kwa wansembe pakhomo pa chihema chamsonkhano. Wansembe apereke imodzi kuti ikhale nsembe yopepesera machimo ndipo ina ikhale nsembe yopsereza. Akatero, ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera mkaziyo pamaso pa Chauta, chifuwa cha matenda ake osamba aja. “Choncho mudzaŵayeretsa Aisraele m'kuipitsidwa kwao, kuti angafe chifukwa chochita tchimo la kudetsa chihema changa, chimene chili pakati pao.” Lamulo limeneli ndi la mwamuna amene ali ndi nthenda yotulutsa mafinya m'thupi mwake, ndiponso la amene ataya pansi mbeu yake yaumuna, imene imamsandutsa woipitsidwa. Lamulo limenelinso ndi la mkazi amene ali ndi matenda osamba. Lamuloli ndi la aliyense, mwamuna kapena mkazi, amene ali ndi nthenda yotulutsa mafinya kumaliseche kwake, ndiponso la mwamuna amene agona ndi mkazi woipitsidwa. Chauta adalankhula ndi Mose pambuyo pa imfa ya ana aŵiri a Aroni omwe adaphedwa, atasendera mosayenera pafupi ndi Chauta. Chauta adauza Mose kuti, “Uza Aroni mbale wako kuti asamaloŵa nthaŵi iliyonse ku malo opatulika kwambiri, kuseri kwa nsalu yochinga, pamaso pa chivundikiro chokhala pamwamba pa Bokosi lachipangano, kuti angafe, chifukwa Ine ndidzaonekera mu mtambo pamwamba pa chivundikirocho. Koma Aroniyo aziloŵa m'malo opatulikawo motere: azitenga mwanawang'ombe wamphongo kuti akhale nsembe yopepesera machimo, ndi nkhosa yamphongo kuti ikhale nsembe yopsereza. Azivala mwinjiro woyera wabafuta, azivalanso kabudula wabafuta ndi kumangira lamba wabafuta, ndipo avalenso nduŵira yabafuta kumutu. Zimenezi ndi zovala zopatulika. Avale zimenezi atasamba thupi lonse. Aroniyo atenge atonde aŵiri ochokera ku mpingo wa Aisraele, kuti akhale nsembe yopepesera machimo, ndi nkhosa imodzi yamphongo kuti ikhale nsembe yopsereza. “Aroni apereke ng'ombe yamphongo kuti ikhale nsembe yopepesera machimo a iye mwiniwake, kuti achite mwambo wopepesera machimo ake ndi a banja lake. Tsono atenge mbuzi ziŵiri zija, ndipo aziike pamaso pa Chauta pakhomo pa chihema chamsonkhano. Pompo Aroni achite maere pa mbuzi ziŵirizo, kuti imodzi ikhale ya Chauta, ndipo ina ikhale ya Azazele. Aroniyo abwere ndi mbuzi imene maere aonetsa kuti ndi ya Chauta, ndipo aipereke kuti ikhale nsembe yopepesera machimo. Koma mbuzi imene maere aonetsa kuti ndi ya Azazele, abwere nayo yamoyo pamaso pa Chauta, kuti achite mwambo wopepesera machimo pa mbuziyo, ndi kuitumiza ku chipululu kwa Azazele. “Aroni apereke ng'ombe yamphongoyo kuti ikhale nsembe yopepesera machimo a iye mwini, ndipo motero achite mwambo wopepesera machimo ake ndi a banja lake. Tsono aphe ng'ombeyo kuti ikhale nsembe yopepesera machimo a iye mwini. Kenaka atenge kambiya kodzaza ndi makala a moto ochokera pa guwa lansembe pamaso pa Chauta, atape lubani wonunkhira ndi woperapera, manja aŵiri, ndipo aloŵe naye kuseri kwa nsalu yochinga. Atatero, athire lubani pa moto pamaso pa Chauta, kuti utsi wa lubaniwo uphimbe chivundikiro chimene chikhala chili pamwamba pa bokosi lachipangano, kuti angafe. Kenaka atengeko magazi ena a ng'ombeyo, aŵawaze ndi chala chake pa chivundikiro cha bokosi lachipangano mbali yakuvuma. Ndiponso awazeko magaziwo kasanu ndi kaŵiri ndi chala chake patsogolo pa chivundikirocho. “Tsono Aroni aphe mbuzi ya nsembe yopepesera machimo a anthu. Magazi ake aloŵe nawo kuseri kwa nsalu yochinga, ndi kuchita nawo monga momwe adachitira ndi magazi a ng'ombe, pakuwaza magaziwo pa chivundikiro chija ndi patsogolo pa chivundikirocho. Akatero ndiye kuti wachita mwambo wopepesera malo oyera chifukwa cha kuipitsidwa kwa Aisraele, ndiponso chifukwa cha kusamvera kwao, ndiye kuti machimo ao onse. Achite chimodzimodzi ndi chihema chamsonkhano chokhala ndi iwo pakati pa machimo ao. Musakhale munthu ndi mmodzi yemwe m'chihema chamsonkhano, pamene Aroni akuloŵa kukachita mwambo wopepesera malo oyera. Musakhale munthu mpaka atamaliza kuchita mwambo wopepesera machimo ake a iye mwini, a banja lake, ndi a mpingo wa Aisraele. Tsono atatuluka Aroniyo apite ku guwa limene lili pamaso pa Chauta ndi kulichitira mwambo wolipepesera. Atengeko magazi a ng'ombe yamphongo ndiponso a mbuzi, ndi kuŵapaka pa nyanga za guwalo molizungulira. Awazeko magazi ena pamwamba pa guwalo ndi chala chake kasanu ndi kaŵiri, kuti alipatule ndi kuliyeretsa pochotsa machimo a Aisraele. “Atamaliza kuchita mwambo wopepesera malo oyera, chihema chamsonkhano pamodzi ndi guwa, wansembeyo apereke mbuzi yamoyo kwa Chauta. Tsono Aroni asanjike manja ake pamutu pa mbuziyo, ndipo aululire pa mbuzi imeneyo zochimwa zonse za Aisraele pamodzi ndi kusamvera kwao konse, ndiye kuti machimo ao onse. Machimowo aŵaike pamutu pa mbuzi ija, ndipo munthu amene adamusankhiratu aithamangitsire ku chipululu mbuziyo. Mbuziyo isenze machimo ao onse ndi kumanka nawo ku chipululu. Munthuyo aileke mbuzi imeneyo kuti ipite ku chipululu. “Kenaka Aroni aloŵe m'chihema chamsonkhano, avule zovala zabafuta zimene adavala pokaloŵa m'malo oyera zija, ndipo azisiye komweko. Asambe thupi lonse ku malo oyera, ndipo avale zovala zake. Atuluke kukapereka nsembe yopsereza ya iye mwini, ndiponso nsembe yopsereza yoperekera anthu. Akatero, ndiye kuti wachita mwambo wopepesera machimo a iye mwini ndi a anthu. Mafuta a nyama ya nsembe yopepesera machimo, aŵatenthere pa guwa. Tsono munthu amene adathamangitsira mbuzi kwa Azazele uja, achape zovala zake ndipo asambe thupi lonse, pambuyo pake aloŵe ku zithando. Ng'ombe ndi mbuzi zoperekera nsembe zopepesera machimo zija, zimene magazi ake adabwera nawo kuti achitire mwambo wopepesera malo oyera, azitulutsire kunja kwa zithando. Zikopa zake, nyama yake ndi ndoŵe yake azitenthe. Munthu amene atenthe zimenezo achape zovala zake, ndipo asambe thupi lonse, tsono pambuyo pake angathe kuloŵa ku zithando. “Limeneli likhale lamulo lanu lamuyaya kuti mwezi wachisanu ndi chiŵiri, pa tsiku lakhumi la mwezi, muzisala zakudya ndipo musagwire ntchito iliyonse, inu mbadwa, ndiponso mlendo wokhala nao pakati panu. Pajatu pa tsiku limenelo padzakhala mwambo wopepesera machimo anu, kuti machimo anu achotsedwe. Choncho mudzakhala oyera pamaso pa Chauta. Limeneli lidzakhala tsiku lanu lalikulu la sabata lopumula, ndipo mudzasale zakudya. Limeneli likhale lamulo lanu lamuyaya. Wansembe amene wadzozedwa nayeretsedwa kuti akhale mkulu wa ansembe onse m'malo mwa bambo wake, adzachite mwambo wopepesera machimo, atavala zovala zopatulika zabafuta. Adzachite mwambo wopepesera malo oyera. Adzachitenso mwambo wopepesera chihema chamsonkhano ndi guwa, ndiponso mwambo wopepesera machimo a ansembe anzake ndi a mpingo wonse. Limeneli lidzakhala lamulo lanu lamuyaya, kuti muzidzachita mwambo wopepesera machimo onse a Aisraele kamodzi pa chaka.” Tsono Mose adachita monga momwe Chauta adamlamulira. Chauta adauza Mose kuti, “Uza Aroni ndi ana ake, pamodzi ndi Aisraele onse, kuti Chauta akulamula kuti, ‘Mwisraele aliyense akapha ng'ombe, kapena mwanawankhosa, kapena mbuzi, ku zithando kapena kunja kwa zithando, koma osabwera nayo pa khomo pa chihema chamsonkhano, kuti ikhale mphatso yopereka kwa Chauta, munthuyo wapalamula mlandu wa magazi, chifukwa wakhetsa magazi. Munthu ameneyo achotsedwe pakati pa anthu anzake. Ndiye kunena kuti Aisraele azitenga nyama zimene akadaphera kwina kwake, afike nazo pamaso pa Chauta kwa wansembe wokhala pakhomo pa chihema chamsonkhano, ndipo aziphere pomweko, kuti zikhale nsembe zachiyanjano. Ndipo wansembe awaze magazi ake pa guwa la Chauta, pakhomo pa chihema chamsonkhano. Atatero atenthe mafuta ake, kuti atulutse fungo lokomera Chauta. Motero nsembe zao asadzapherenso milungu yachabe imene amadziipitsa nayo. Limeneli likhale lamulo lao lamuyaya pa mibadwo yonse.’ “Uŵauze kuti, ‘Mwisraele aliyense, kapena mlendo amene amakhala pakati pao, wopereka nsembe yopsereza kapena nsembe ina iliyonse, akapanda kubwera nayo pakhomo pa chihema chamsonkhano kudzaipereka pamaso pa Chauta, munthu ameneyo achotsedwe pakati pa anthu anzake.’ “Mwisraele aliyense, kapena mlendo wokhala pakati pao, akadya magazi, ndidzamfulatira ndi kumchotsa pakati pa anthu anzake. Pakuti moyo wake wa cholengedwa chilichonse uli m'magazi, ndipo ndaŵapereka kwa inu kuti muzichitira mwambo wopepesera machimo a moyo wanu pa guwa. Pajatu magazi ndiwo amene amachotsa machimo, chifukwa cha moyo umene umakhala m'magazimo. Nchifukwa chake ndaŵauza Aisraele kuti munthu aliyense mwa inu, kapena mlendo wokhala pakati panu, asadye magazi. Ndipo Aisraele onse kapena alendo okhala pakati pao, amene amapha ku uzimba nyama kapena mbalame zimene amadya, ataye magazi ake pansi ndi kuŵakwirira ndi dothi. “Pajatu moyo wa cholengedwa chilichonse uli m'magazi mwake. Nchifukwa chake ndaŵauza Aisraele kuti, ‘Musadye magazi a cholengedwa chilichonse, pakuti moyo wa cholengedwa chilichonse uli m'magazi mwakemo. Aliyense wodya magazi adzachotsedwa. Munthu aliyense wodya chinthu chofa chokha, kapena chojiwa ndi chilombo, ngakhale akhale mbadwa kapena mlendo, achape zovala zake, ndipo asambe thupi lonse, koma akhalabe woipitsidwa mpaka madzulo, ndipo pambuyo pake adzakhala woyeretsedwa. Koma akapanda kuchapa zovalazo, kapena akapanda kusamba thupi lonse, adzasenza machimo ake.’ ” Chauta adauza Mose kuti, “Uza Aisraele kuti, Ine ndine Chauta, Mulungu wanu. Musamachita zimene amachita anthu a ku Ejipito kumene munkakhala kuja, ndiponso musadzachite zimene amachita anthu a ku Kanani kumene ndikukufikitsaniko. Musatsate miyambo yao. Muzichita zimene ndikukulamulani, ndi kutsata malamulo anga ndi kuŵamvera. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu. Nchifukwa chake muchite zimene ndikukulamulani ndipo muzimvera malamulo anga, motero mudzakhala ndi moyo. Ine ndine Chauta. “Munthu wina aliyense mwa inu asagone ndi wachibale wake. Ine ndine Chauta. Usachititse manyazi bambo wako pakugona ndi mai wako. Ameneyo ndi mai wako, usamchititse manyazi. Usachititse manyazi bambo wako pakugona ndi mkazi wake aliyense. Usagone ndi mlongo wako, mwana wamkazi wa bambo wako, kapena mwana wamkazi wa mai wako, ngakhale abadwire kwanu kapena kuchilendo. Usagone ndi mdzukulu wako, mwana wa mwana wako wamwamuna, kapena mdzukulu wako, mwana wa mwana wako wamkazi, chifukwa kuteroko nkudzivula. Usagone ndi mwana wamkazi wa mkazi wa bambo wako amene bambo wakoyo adabala, poti ameneyo ndi mlongo wako. Usagone ndi mlongo wa bambo wako, poti ameneyo ndi thupi limodzi ndi bambo wako. Usagone ndi mbale wa mai wako, poti ameneyo ndi thupi limodzi ndi mai wako. Usagone ndi mkazi wa mbale wa bambo wako, poti ameneyo ndi mai wako. Usagone ndi mkazi wa mwana wako, poti ameneyo ndi mpongozi wako. Usagone ndi mkazi wa mbale wako, chifukwa kuteroko nkuvula mbale wako. Usagone ndi mkazi ndiponso ndi mwana wamkazi wa mkaziyo, ndipo usagone ndi mwana wamkazi wa mwana wake wamwamuna, kapena mwana wamkazi wa mwana wake wamkazi. Amenewo ndi thupi lake la mkaziyo, ndipo kuteroko nkuchita chinthu choipa kwambiri. Ndipo usakwatire mbale wa mkazi wako ndi kumuvula pamene mbale wako ali moyo. “Usayandikire mkazi kuti umvule pamene ali wosamba. Usagone ndi mkazi wa mnzako ndi kudziipitsa naye. Usatenge mwana wako aliyense kuti umpereke ngati nsembe yamoto kwa Moleki, kuti ungaipitse dzina la Mulungu wako. Ine ndine Chauta. Usagone ndi mwamuna ngati mkazi. Chimenecho ndi chinthu chonyansa. Ndipo usagone ndi nyama ndi kudziipitsa nayo, ngakhalenso mkazi aliyense asadzipereke kwa nyama kuti agone nayo, pakuti chimenecho ndi chisokonezo choopsa. “Musadziipitse ndi zinthu zimenezi, chifukwa mitundu ina ya anthu amene ndikuipirikitsa inu mukubwera, idadziipitsa ndi zoipa zoterezi. Dziko lidaipa kotero kuti ndidalanga tchimo lake, ndipo dzikolo lidasanza anthu ake okhalamo. Koma inuyo mutsate malamulo anga ndi kuchita zimene ndikukulamulani. Musachite chilichonse mwa zonyansazi, ngakhale inu mbadwanu kapena mlendo wokhala pakati panu. Pajatu anthu am'dzikomo amene adaalipo inu musanafike, ankachita zonyansa zonsezi, kotero kuti dziko lidaipitsidwa. Musachite zimenezi kuti dziko lingakusanzeni mukaliipitsa, monga momwe lidasanzira mtundu wa anthu umene udaalipo m'dzikomo, inu musanafike. Pakuti aliyense amene adzachita zonyansa zimenezi, adzachotsedwa pakati pa anthu anzake. Tsono mverani malamulo anga oletsa kutsata zonyansa zimene anthu ankazichita, inu musanafike. Musadziipitse nazo konse. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.” Chauta adauzanso Mose kuti, “Uza mpingo wonse wa Aisraele kuti, ‘Mukhale oyera pakuti Ine Chauta, Mulungu wanu, ndine woyera. Aliyense mwa inu aziwopa mai wake ndi bambo wake. Muzisunga masiku anga a Sabata, Ine ndine Chauta, Mulungu wanu. Musabwerere ku mafano, kapena kudzipangira nokha milungu ya zitsulo zosungunula. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.’ “Mukamapereka nsembe yachiyanjano kwa Chauta, Mulungu wanu, muchite mwa njira yoti mulandiridwe. Muidye tsiku lomwe mwaiperekalo, kapena m'maŵa mwake, koma zotsalako mpaka pa tsiku lachitatu muzitenthe. Mukaidya pa tsiku lachitatu, kuteroko nkuchita chinthu chonyansa, ndipo nsembeyo sidzalandiridwa. Munthu aliyense amene aidye, adzasenza tchimo lake chifukwa chakuti waipitsa chinthu choyera cha Chauta. Munthu ameneyo achotsedwe pakati pa anthu anzake. “Pamene mukolola m'minda mwanu, musakolole munda wanu mpaka m'malire mwenimweni, ndipo musatolenso khunkha lake. Musakolole mphesa zonse m'munda wanu wamphesa, ndipo musatolenso mphesa zakugwa m'munda mwanumo. Zimenezo musiyire anthu osauka ndiponso alendo, Ine ndine Chauta, Mulungu wanu. “Musabe, musachite zinthu zonyenga, ndipo musaname. Musalumbire m'dzina langa monyenga ndi kumaipitsa dzina la Ine Mulungu wanu pakutero. Ine ndine Chauta. “Musachenjeretse mnzanu kapena kumubera zinthu zake. Musasunge malipiro a munthu wantchito usiku wonse mpaka m'maŵa. Musatemberere gonthi, kapena kumuikira chokhumudwitsa munthu wakhungu. Koma muziwopa Mulungu wanu, Ine ndine Chauta. “Musamaweruza mopanda chilungamo. Musachite tsankho pakati pa anthu osoŵa ndi anthu otchuka, koma muziweruza mnzanu mwachilungamo. Musamangoyendayenda uku ndi uku kumachita ukazitape pakati pa anthu a mtundu wanu. Musachite kanthu kalikonse kamene kangathe kudzetsa imfa ya munthu wina. Ine ndine Chauta. “Musadane ndi mbale wanu mumtima mwanu, koma mumdzudzule mosabisa kuti mungavomerezane naye pa tchimo lake. Musabwezere choipa, ndipo musakwiyire anthu a mtundu wanu, koma mukonde mnzanu monga momwe mumadzikondera inu nomwe. Ine ndine Chauta. “Muzitsata malamulo anga. Musalole kuti ng'ombe zanu zikwerane ndi zoŵeta za mtundu wina. Musafese mbeu za mitundu iŵiri m'munda mwanu, ndipo musavale chovala chopangidwa ndi nsalu za mitundu iŵiri. “Munthu akagona ndi mkazi amene ali mdzakazi wofunsidwa mbeta ndi munthu wina, koma wosaomboledwa kapenanso asanalandire ufulu wake, aimbidwe mlandu. Onsewo asaphedwe, chifukwa mkaziyo anali asanalandire ufulu wake. Koma mwamunayo abwere ndi nsembe yopepesera kupalamula kwake pamaso pa Chauta, pakhomo pa chihema chamsonkhano. Nsembe yopepesera kupalamulayo ikhale nkhosa yamphongo. Wansembe achite mwambo wopepesera machimo a munthuyo ndi nkhosa yamphongo ya nsembe yopepesera kupalamulayo pamaso pa Chauta, chifukwa cha tchimo limene munthuyo adachita, ndipo tchimo adachitalo lidzakhululukidwa. “Pamene muloŵa m'dzikomo ndi kubzala mitengo yamitundumitundu ya zipatso, zipatsozo zikhale zoletsedwa. Zikhale zoletsedwa kwa inu zaka zitatu, musadye pa nthaŵi imeneyo. Pa chaka chachinai, zipatso zonse zidzakhala zopatulikira Chauta ngati nsembe yomtamandira. Koma pa chaka chachisanu mudzatha kudya zipatso zake, kuti choncho mitengoyo idzakubalireni kwambiri. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu. “Musadye nyama yamagazi. Musamaombeza kapena kuchita zaufiti. Musamamete mduliro kapena kumeta m'mphepete mwa ndevu zanu. Musadzichekecheke pa thupi lanu chifukwa cha munthu wakufa kapena kudzitema mphini za mtundu uliwonse. Ine ndine Chauta. “Musaipitse mwana wanu wamkazi pakumsandutsa mkazi wachiwerewere kuti dziko lingasanduke la anthu adama ndi loipa kwambiri. Muzisunga masiku anga a Sabata ndi kulemekeza malo anga oyera, Ine ndine Chauta. “Musamapita kwa anthu olankhula ndi mizimu ya anthu akufa, kapena kwa anyanga. Musaŵafunefune kuti angakuipitseni. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu. “Muzikhala mwaulemu pamaso pa munthu waimvi. Wokalamba muzimchitira ulemu, ndipo pakutero mudzaopa Mulungu wanu. Ine ndine Chauta. “Pamene mlendo akhala nanu m'dziko mwanu, musamchite choipa. Mlendo amene akhala nanu, akhale ngati mbadwa pakati panu, ndipo mumkonde monga momwe mumadzikondera inu nomwe. Pajatu inunso mudaali alendo m'dziko la Ejipito. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu. “Musamaweruza milandu molakwa, ndipo muyeso wanu woyesera utali wa zinthu, kulemera kwa zinthu kapena kuchuluka kwa zinthu, usamakhala wonyenga. Miyeso yanu ya sikelo, miyeso yoyesera kulemera kwa zinthu, miyeso yotchedwa efa ndi hini izikhala yolungama. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu, amene ndidakutulutsani ku dziko la Ejipito. Muzimvera malamulo anga onse, muzichita monga momwe ndidakulamulirani, malamulowo muziŵatsata. Ine ndine Chauta.” Chauta adauza Mose kuti, “Uza Aisraele kuti: Mwisraele aliyense, kapena mlendo wokhala nao m'dziko mwanu, akapereka ana ake kwa Moleki, aphedwe: anthu am'dzikomo amponye miyala. Munthu ameneyo ndidzamfulatira, ndipo ndidzamchotsa pakati pa anthu anzake, chifukwa wapereka ana ake kwa Moleki ndi kuipitsa malo anga oyera, ndiponso waipitsa dzina langa loyera. Anthu am'dzikomo akachita ngati sakumuwona munthuyo, pamene akupereka mmodzi mwa ana ake kwa Moleki, namleka osamupha, Ineyo ndidzamfulatira munthu ameneyo ndi banja lake lonse. Ndidzaŵachotsa pakati pa anthu anzao, pamodzi ndi onse amene amaŵatsanzira nadziipitsa pakupembedza Moleki. “Munthu akapita kwa wolankhula ndi mizimu yoipa ndi kwa wanyanga, nadziipitsa pakutsatira iwowo, ndidzamfulatira ndipo ndidzamchotsa pakati pa anthu anzake. Nchifukwa chake mudziyeretse, ndipo mukhale oyera, poti Ine ndine Chauta, Mulungu wanu. Muzimvera malamulo anga ndi kuŵatsata. Ine ndine Chauta amene ndikukuyeretsani. Munthu aliyense wotemberera bambo wake ndi mai wake ayenera kuphedwa. Munthu ameneyo watemberera bambo wake ndi mai wake, tsono magazi ake akhale pa iyeyo. “Munthu akachita chigololo ndi mkazi wa mwiniwake, mwamunayo pamodzi ndi mkaziyo onsewo aphedwe. Munthu wogona ndi mkazi wa bambo wake, wavula bambo wake, ndipo onsewo ayenera kuphedwa. Magazi ao akhale pa iwowo. Munthu akagona ndi mkazi wa mwana wake, onsewo ayenera kuphedwa. Iwowo achita chigololo pachibale, ndipo magazi ao akhale pa iwowo. Munthu akagona ndi munthu wamwamuna mnzake ngati mkazi, onsewo achita chinthu chonyansa, ndipo ayenera kuphedwa. Magazi ao akhale pa iwowo. Munthu akakwatira mkazi, nakwatiranso mai wake wa mkaziyo, kuteroko nkuchita chinthu choipa kwambiri. Onsewo ayenera kuŵatentha pa moto, mwamunayo pamodzi ndi akazi omwewo, kuti chinthu choipa kwambiri chotere chisapezeke pakati panu. Mwamuna akagona ndi nyama, ayenera kuphedwa, ndipo nyamayo muiphenso. Mkazi akagona ndi nyama, aphedwe pamodzi ndi nyamayo. Aphedwe ndipo magazi ao akhale pa mkaziyo ndi nyamayo. “Munthu akakwatira mlongo wake, mwana wamkazi wa bambo wake, kapena mwana wamkazi wa mai wake, onse aŵiriwo achita chinthu chochititsa manyazi, ndipo onsewo aphedwe pakhamu pa anthu a mtundu wao. Chifukwa aphwanya malamulo motero, alipire choipa chake. Munthu akagona ndi mkazi wosamba, ndiye kuti wavula msambo wake, nayenso mkaziyo wadzivula. Onse aŵiriwo achotsedwe pakati pa anthu anzao. Musavule mbale wa mai wanu kapena mlongo wa bambo wanu, poti kuteroko nkuvula wa pa chibale chanu. Onse aŵiriwo adzalipira machimo ao. Munthu akagona ndi mkazi wa mbale wa bambo wake, wavula mbale wa bambo wake. Onse aŵiriwo adzasenza machimo ao ndipo adzafa opanda ana. Munthu akakwatira mkazi wa mbale wake, ndiye kuti wachita chinthu chonyansa. Wavula mbale wake, ndipo onse aŵiriwo adzakhala opanda ana. “Nchifukwa chake muzisunga malamulo anga, ndipo muzichita zonse zimene ndimakulamulani ndi kuzitsata, kuti dziko limene mukupita kuti mukakhalemolo lingakudeni. Musatsanzire miyambo ya mtundu wa anthu amene ndikuupirikitsa inu mukufika. Iwo ankachita zimenezi, nchifukwa chake ndidanyansidwa nawo kwambiri. Koma inuyo ndakuuzani kuti: Mudzalandira dziko lao, ndipo ndidzakupatsani dzikolo kuti likhale lanu, dziko lake lamwanaalirenji. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu, amene ndakupatulani pakati pa mitundu yonse ya anthu. Nchifukwa chake muzisiyanitsa pakati pa nyama zoipitsidwa ndi zosaipitsidwa, pakati pa mbalame zosaipitsidwa ndi zoipitsidwa. Musadziipitse pakudya nyama kapena mbalame, kapenanso zinthu zilizonse zimene zadzaza pansi pano, zomwe ndazipatula kuti inu muzidziŵe kuti nzoipitsidwa. Muzikhala oyera pamaso panga, pakuti Ine Chauta ndine woyera, ndipo ndakupatulani pakati pa anthu onse kuti mukhale anthu anga. “Mwamuna kapena mkazi wolankhula ndi mizimu ya anthu akufa, kapena munthu wanyanga, ayenera kuphedwa. Aŵaponye miyala, ndipo magazi ao akhale pa iwowo.” Chauta adauza Mose kuti, “Ulankhule ndi ansembe, ana a Aroni, ndipo uŵauze kuti: Pasapezeke ndi mmodzi yemwe amene adziipitse pokhudza munthu wakufa pakati pa abale ake. Koma angathe kukhudza mai wake, bambo wake, mwana wake wamwamuna, mwana wake wamkazi, kapena mlongo wake wosakwatiwa amene amakhala pafupi naye, poti chikhalire alibe mwamuna. Wansembe asadziipitse pa imfa ya munthu amene wakwatira naye ku banja limodzi. Ansembe asamete tsitsi kumutu kwao, kapena kumeta m'mphepete mwa ndevu zao, kapenanso kudzichekacheka pa thupi. Akhale oyera pamaso pa Ine Mulungu, ndipo asachititse manyazi dzina langa. Amapereka nsembe zotentha pa moto, chakudya cha Mulungu wao, nchifukwa chake azikhala oyera. Asakwatire mkazi wachiwerewere kapena mkazi amene wadziipitsa, ndiponso asakwatire mkazi amene mwamuna wake wamsudzula, pakuti wansembe ndi woyera pamaso pa Mulungu wake. Akhale munthu woyera kwa inu, chifukwa amapereka chakudya cha Mulungu wanu. Akhale munthu woyera kwa inu, chifukwa Ine Chauta amene ndimakuyeretsani, ndine woyera. Ndipo mwana wamkazi wa wansembe aliyense akadziipitsa pokhala wachiwerewere, amaipitsa bambo wake. Mwanayo ayenera kumtentha pa moto. “Munthu amene ali mkulu wa ansembe onse, amene adamdzoza pa mutu ndi mafuta, ndiponso amene adapatulidwa pakumuveka zovala zaunsembe, asalekerere tsitsi lake, kapena kung'amba zovala zake kusonyeza kuti ali pamaliro. Asakaloŵe kumene kuli munthu wakufa aliyense ndi kudziipitsa, ngakhale mtembo wa bambo wake kapena wa mai wake. Asatuluke m'malo oyera kapena kuipitsa malo oyera a Mulungu wake, pakuti mafuta odzozera a Mulungu wake amene adamdzoza nawo ali pa iye. Ine ndine Chauta. Ndipo akwatire mnamwali wosadziŵa mwamuna, asakwatire mkazi wamasiye kapena mkazi wosudzulidwa, kapenanso mkazi wachiwerewere. Koma akwatire mnamwali wosadziŵa mwamuna pakati pa anthu a mtundu wake, amene sanadziŵeko mwamuna, kuti asaloŵetse mtundu wosayera pakati pa ana ake, pakuti Ine ndine Chauta amene ndinamuyeretsa.” Chauta adauza Mose kuti, “Uza Aroni kuti munthu aliyense mwa zidzukulu zake pa mibadwo yonse, amene ali ndi chilema, asabwere kudzapereka nsembe kwa Mulungu wake. Munthu aliyense wachilema sayenera kusendera pafupi, monga munthu wakhungu kapena wopunduka miyendo, munthu wopunduka nkhope kapena wokhala ndi chiwalo china chachitali dziŵi, munthu wa phazi lopunduka kapena wa dzanja lopunduka, munthu wanundu kapena kafupidolo, munthu wa maso opunduka, munthu wa nthenda yonyerenyesa, kapena wamphere, kapenanso wotswanyika mavalo. Mwa zidzukulu za wansembe Aroni pasadzapezeke munthu ndi mmodzi yemwe wokhala ndi chilema, amene adzapereke nsembe zopsereza kwa Chauta. Popeza kuti ali ndi chilema, sayenera kusendera pafupi ndi guwa kuti akapereke zakudya za Mulungu wake. Koma angathe kudya chakudya choperekedwa kwa Mulungu wake, buledi wopatulika kopambana uja, pamodzi ndi zotsalira zopatulika za nsembe. Koma asadzabwere pafupi ndi nsalu yochinga, kapena kuyandikira guwa, chifukwa ali ndi chilema, kuwopa kuti angadzaipitse malo anga oyera. Pakuti Ine ndine Chauta amene ndidapatula malo amenewo.” Zimenezi ndizo zimene Mose adauza Aroni ndi ana ake aamuna ndiponso Aisraele onse. Chauta adauza Mose kuti, “Uza Aroni pamodzi ndi ana ake aamuna kuti azilemekeza zinthu zopatulika zimene Aisraele amapereka kwa Ine, kuti angaipitse dzina langa loyera. Ine ndine Chauta. Munthu wina aliyense mwa zidzukulu zake pa mibadwo yonse, akayandikira zopatulika zimene Aisraele adazipereka kwa Chauta, pamene iyeyo ali woipitsidwa, asaonekenso pamaso panga. Ine ndine Chauta. Munthu aliyense mwa zidzukulu za Aroni amene ali ndi khate kapena amene amatulutsa zoipa m'thupi mwake, asadyeko zinthu zopatulika mpaka atayeretsedwa. Mwina wansembe angathe kukhudza chinthu choipitsidwa chifukwa chokhudzana ndi chinthu chakufa, kapena angathe kutaya mbeu yake yaumuna. Mwina angathe kukhudza kachilombo kokwaŵa, kamene kangathe kumuipitsa, kapena kukhudza munthu amene angathe kumuipitsa mwa mtundu uliwonse. Wansembe aliyense wokhudza chinthu chotere, akhala woipitsidwa mpaka madzulo, ndipo asadyeko zinthu zopatulika mpaka atasamba thupi lonse. Adzakhala woyeretsedwa dzuŵa litaloŵa, ndipo pambuyo pake adzatha kudyako zinthu zopatulikazo, poti zimenezo ndi chakudya chake. Asadye chinthu chofa chokha kapena chojiwa ndi chilombo, ndi kumadziipitsa nazo zimenezo. Ine ndine Chauta. Nchifukwa chake ansembe asunge malamulo anga kuti angachimwe ndipo angafe chifukwa choŵaphwanya. Ine ndine Chauta, amene ndimaŵayeretsa. “Wapadera asadyeko zinthu zopatulika. Mlendo wongokhala nao kwa wansembe, kapena wantchito wake, asadyeko chinthu chopatulika. Koma wansembe akagula kapolo ndi ndalama kuti akhale wake, kapoloyo angathe kudya nao zinthuzo. Ndipo onse amene abadwa m'nyumba mwa wansembe angathe kudyako chakudya chake. Mwana wamkazi wa wansembe akakwatiwa ndi wapadera, asadyeko zopereka zopatulikazo. Koma mwana wamkazi wa wansembeyo akakhala wamasiye kapena wosudzulidwa, ndipo alibe mwana, nabwerera ku nyumba ya bambo wake monga pa nthaŵi ya utsikana wake, angathe kudyako chakudya cha bambo wake. Koma wapadera asadyeko. Munthu wapadera akadyako chinthu chopatulika mosadziŵa, alipire wansembe chifukwa cha chinthucho, ndipo aonjezepo chimodzi mwa zigawo zisanu za mtengo wake. Ansembe asaipitse nsembe zopatulika za Aisraele zimene amazipereka kwa Chauta. Asachimwitse ndi kupalamulitsa Aisraelewo pakuŵalola kudya zakudya zao zopatulika. Inetu ndine Chauta, amene ndimazipatula.” Chauta adauza Mose kuti, “Uza Aroni, ana ake ndi Aisraele onse kuti, mwina munthu wa m'banja la Aisraele, kapena mlendo wokhala m'dziko la Israele, adzabwera ndi chopereka chake kuti aperekere chimene wachilumbirira. Mwina adzabwera ndi chopereka kuti chikhale nsembe yaufulu yopereka kwa Chauta ngati nsembe yopsereza. Kuti nsembeyo ilandiridwe, apereke nyama yopanda chilema kaya ndi ng'ombe yamphongo, kapena nkhosa yamphongo kapenanso tonde. Musapereke nyama iliyonse yachilema, chifukwa Chauta sadzakulandirani. Mwina munthu wina adzapereka nsembe yachiyanjano kwa Chauta, kuti achitedi zimene adalumbirira, kapena kuti ikhale nsembe yaufulu. Ngati ndi ng'ombe kapena nkhosa, kuti Chauta ailandire, iyenera kukhala yopanda chilema. Musapereka kwa Chauta nyama zakhungu kapena zopunduka, kapena zoduka chiwalo, kapena zotulutsa mafinya m'thupi, kapena za nthenda zonyerenyesa, kapena zamphere. Nyama zotere asazipereke kwa Chauta, zisakhale nsembe zopsereza pa guwa la Chauta. Mungathe kupereka ng'ombe yamphongo kapena nkhosa imene ili ndi chiwalo chachitali kapena chachifupi, kuti ikhale nsembe yaufulu, koma ikakhala nsembe yolumbirira, singathe kulandiridwa. Nyama iliyonse imene mavalo ake ali onyuka kapena otswanyika, kapena ong'ambika kapena oduka, musaipereke ngati nsembe kwa Chauta m'dziko mwanu. Ndipo musapereke nyama iliyonse ya mtundu umenewo imene mwailandira kwa mlendo, kuti ikhale nsembe ya chakudya chopereka kwa Chauta. Zimenezi sadzazilandira chifukwa zili ndi chilema ndipo nzopunduka.” Chauta adauza Mose kuti, “Ng'ombe, nkhosa kapena mbuzi ikabadwa, ikhale ndi make masiku asanu ndi aŵiri. Ndipo kuyambira pa tsiku lachisanu ndi chitatu mpaka m'tsogolo mwake, ingathe kulandiridwa kuti ikhale nsembe yopsereza, yopereka kwa Chauta. Make akakhala ng'ombe kapena nkhosa, musaphe makeyo pamodzi ndi mwana wake tsiku limodzi. Pamene mupereka nsembe yothokoza Chauta, muipereke mwa njira yoti ilandiridwe. Muidye pa tsiku lomwelo, ndipo musaisiyeko mpaka m'maŵa. Ine ndine Chauta. “Tsono muzimvera malamulo anga ndi kuŵatsata. Ine ndine Chauta. Musanyoze dzina langa loyera, koma likhale lolemekezeka pakati pa Aisraele. Ine ndine Chauta, amene ndimakuyeretsani, ndipo ndidakutulutsani ku dziko la Ejipito, kuti ndikhale Mulungu wanu. Ine ndine Chauta.” Chauta adauza Mose kuti, “Uza Aisraele kuti, ‘Masiku achikondwerero osankhidwa olemekeza Chauta, amene mudzaŵalengeza kuti akhale masiku oyera amisonkhano, masiku achikondwerero amene Ine ndaŵasankha, ndi aŵa: pa masiku asanu ndi limodzi muzigwira ntchito, koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi tsiku lalikulu la Sabata, lopumula, tsiku la msonkhano wopatulika. Musamagwira ntchito iliyonse. Limenelo likhale tsiku la Sabata la Chauta kulikonse kumene mukakhale.’ “Masiku achikondwerero osankhidwa a Chauta, masiku oyera amisonkhano amene mudzaŵalengeza pa nthaŵi yake, ndi aŵa: pa mwezi woyamba, tsiku la 14 la mweziwo, madzulo ake, ndi tsiku la Paska ya Chauta. Ndipo tsiku la 15 la mwezi womwewo ndi tsiku la chikondwerero cha buledi wosafufumitsa, lolemekezera Chauta. Pa masiku asanu ndi aŵiri muzidya buledi wosafufumitsa. Pa tsiku loyamba muchite msonkhano wopatulika, musagwire ntchito yotopetsa. Koma mupereke nsembe yopsereza kwa Chauta pa masiku asanu ndi aŵiri. Tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi tsiku la msonkhano wopatulika, musagwire ntchito zotopetsa.” Chauta adauzanso Mose kuti, “Uza Aisraele kuti, ‘Mukakaloŵa m'dziko limene ndikukupatsanilo ndi kukakolola za m'minda mwanu, mudzabwere kwa wansembe ndi mtolo wa zoyambirira kucha mwa zokolola zanu. Wansembeyo auweyule mtolowo pamaso pa Chauta, kuti inuyo mulandiridwe. Auweyule tsiku lotsatana ndi la Sabata. Pa tsiku limene muweyule mtolowo, muperekenso mwanawankhosa wamphongo wa chaka chimodzi wopanda chilema, kuti akhale nsembe yopsereza yopereka kwa Chauta. Chopereka cha chakudya yopereka pamodzi ndi nkhosayo ikhale makilogaramu aŵiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, kuti ikhale nsembe yopsereza yopereka kwa Chauta, ya fungo lokoma. Ndipo chopereka cha chakumwa yopereka pamodzi ndi nkhosayo, ikhale ya vinyo wokwanira ngati lita limodzi. Musadye buledi kapena tirigu wouma kapena wamuŵisi tsikuli lisanafike, mpaka mutabwera nayo nsembe kwa Mulungu wanu. Limeneli ndilo lamulo lamuyaya pa mibadwo yanu yonse kulikonse kumene mukakhale.’ “Kuyambira tsiku lotsatana ndi la Sabata lija, pamene mudadzapereka mtolo wanu uja wa chopereka choweyula pamaso pa Chauta, muŵerenge milungu isanu ndi iŵiri yathunthu, ndiye kuti masiku asanu mpaka tsiku lotsatana ndi la Sabata lachisanu ndi chiŵiri. Patapita masiku amenewo, mupereke chopereka cha chakudya chatsopano kwa Chauta. M'nyumba mwanu mutenge buledi muŵiri wa ufa wokwanira makilogaramu aŵiri, kuti amuweyule. Akhale wa ufa wosalala, ndipo aphikidwe ndi chofufumitsira, kuti akhale mphatso yoyamba yopereka kwa Chauta. Pamodzi ndi bulediyo, muperekenso anaankhosa asanu ndi aŵiri a chaka chimodzi opanda chilema, ndi likonyani lang'ombe lamphongo ndi nkhosa ziŵiri zamphongo. Zimenezi zikhale nsembe zopsereza zopereka kwa Chauta, pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndiponso chopereka cha chakumwa. Zonsezo zikhale nsembe yopsereza ya fungo lokomera Chauta. Muperekenso tonde mmodzi ngati nsembe yopepesera machimo, ndi anaankhosa aŵiri amphongo a chaka chimodzi ngati nsembe yachiyanjano. Wansembe aziweyule, pamodzi ndi buledi wa mphatso yoyamba uja, kuti zikhale zopereka zoweyula pamaso pa Chauta, pamodzi ndi anaankhosa amphongo aŵiri aja. Zimenezi ndi zopatulika zopereka kwa Chauta zokhalira ansembe. Tsono pa tsiku lomwelo mulengeze, ndipo muchite msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito zotopetsa. Limeneli likhale lamulo lamuyaya kulikonse kumene mukakhale pa mibadwo yanu yonse. “Pamene mukolola dzinthu m'dziko mwanu, musakolole munda wanu mpaka m'malire mwenimweni, ndipo musatole khunkha lake. Zimenezo musiyire anthu osauka ndiponso alendo. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.” Chauta adauza Mose kuti, “Uza Aisraele kuti, ‘Pa mwezi wachisanu ndi chiŵiri, tsiku loyamba la mweziwo, muzilisunga kuti likhale tsiku lalikulu lopumula, tsiku lachikumbutso, lolengezedwa ndi malipenga, tsiku la msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito zotopetsa, ndipo mupereke nsembe yopsereza kwa Chauta.’ ” “Chauta adauza Mose kuti, ‘Tsiku lakhumi la mwezi wachisanu ndi chiŵiri ndi tsiku lochita mwambo wopepesera machimo. Imeneyo ikhale nthaŵi yanu yochita msonkhano wopatulika. Musale zakudya, ndipo mupereke nsembe yopsereza kwa Chauta. Musagwire ntchito pa tsiku limeneli, chifukwa ndi tsiku lochita mwambo wopepesera, wopepeseradi machimo anu pamaso pa Chauta, Mulungu wanu. Aliyense amene sasala zakudya pa tsiku limeneli ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu a mtundu wake. Aliyense amene agwire ntchito pa tsiku limeneli, ndidzamuwononga ameneyo pakati pa anthu a mtundu wake. Musagwire ntchito iliyonse. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibadwo yanu yonse kulikonse kumene mukakhale. Likhale ngati tsiku lalikulu la Sabata lopumula kwa inu, ndipo musale zakudya. Pa tsiku lachisanu ndi chinai la mwezi, kuyambira madzulo ake mpaka madzulo ena otsatira, musunge tsikulo monga ngati la Sabata.’ ” Chauta adauza Mose kuti, “Uza Aisraele kuti, ‘Kuyambira pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiŵiri, pa masiku asanu ndi aŵiri, pazikhala chikondwerero chamisasa cholemekeza Chauta. Pa tsiku loyamba pazikhala msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito zotopetsa. Pa masiku asanu ndi aŵiri muzipereka nsembe zopsereza kwa Chauta. Pa tsiku lachisanu ndi chitatu muzichita msonkhano wopatulika ndi kupereka nsembe yopsereza kwa Chauta. Umenewu ndi msonkhano waukulu. Musagwire ntchito zotopetsa.’ “Ameneŵa ndi masiku achikondwerero osankhidwa olemekeza Chauta, amene muziŵalengeza kuti ndi nthaŵi ya msonkhano wopatulika. Masiku ameneŵa muzipereka kwa Chauta nsembe zapamoto, monga nsembe zopsereza, nsembe zaufa, nsembe zanyama, ndi zopereka za chakumwa, iliyonse pa tsiku lake. Mupereke zimenezo pamodzi ndi nsembe za pa tsiku la Sabata la Chauta, mphatso zanu, nsembe zanu zonse zolumbirira ndi nsembe zanu zonse zaufulu, zimene mumapereka kwa Chauta. “Pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiŵiri, mutakolola dzinthu m'dziko mwanu, muchite chikondwerero cha Chauta pa masiku asanu ndi aŵiri. Tsiku loyamba likhale tsiku lalikulu lopumula, ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu likhalenso tsiku lalikulu lopumula. Pa tsiku loyamba mutenge zipatso zabwino ndithu, nthambi za kanjedza, nthambi zazikulu za mitengo ya masamba ambiri, ndi za misondodzi yakumtsinje, ndipo mukondwere pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, masiku asanu ndi aŵiri. Chaka chilichonse, masiku asanu ndi aŵiriwo musamale kuti akhale achikondwerero, olemekeza Chauta. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibadwo yonse. Muzilisunga pa mwezi wachisanu ndi chiŵiri. Muzikhala m'misasa masiku asanu ndi aŵiri. Onse amene ali mbadwa m'dziko la Israele azikhala m'misasa, kuti mibadwo yanu idzadziŵe kuti ndine amene ndidakhalitsa Aisraele m'misasa, pamene ndidaŵatulutsa ku dziko la Ejipito. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.” Umu ndimo m'mene Mose adafotokozera kwa Aisraele za masiku achikondwerero osankhidwa, olemekeza Chauta. Chauta adauza Mose kuti, “Lamula Aisraele kuti akupatse mafuta anyale, a olivi wabwino kwambiri, kuti nyale izikhala yoyaka nthaŵi zonse m'Nyumba mwanga. Aroni aiyatse nyaleyo pamaso pa Chauta kunja kwa nsalu yochinga bokosi lachipangano, limene lili m'chihema chamsonkhano, kuti ikhale chiyakire kuyambira madzulo mpaka m'maŵa. Limeneli likhale lamulo lamuyaya pa mibadwo yanu yonse. Aroni ayatse nyale zimene zili pa choikapo chake cha golide wabwino kwambiri, kuti zikhale zoyaka nthaŵi zonse pamaso pa Chauta. “Mutenge ufa wosalala, ndipo muphike makeke khumi ndi aŵiri. Keke iliyonse ikhale ya ufa wokwanira makilogaramu aŵiri. Muŵaike m'mizere iŵiri pa tebulo la golide wabwino kwambiri, mzere uliwonse ukhale wa makeke asanu ndi imodzi. Pa mzere uliwonse muikepo lubani wokoma, kuti pamodzi ndi bulediyo akhale chikumbutso cha nsembe yopsereza yopereka kwa Chauta. Pa tsiku la Sabata lililonse Aroni aziika makeke a nsembeyo mosalephera pamaso pa Chauta m'malo mwa Aisraele, kuti chikhale chipangano chamuyaya. Chakudyacho chikhale cha Aroni ndi ana ake, ndipo achidyere m'malo oyera, pakuti kwa iyeyo chimenecho nchopatulika kopambana, chochokera pa nsembe yopsereza kwa Chauta. Lamuloli ndi lamuyaya.” Tsiku lina munthu wina amene mai wake anali Wachiisraele, koma bambo wake anali wa ku Ejipito, adapita kwa Aisraele ndipo adakangana ndi Mwisraele mmodzi ku mahema. Munthu uja adanyoza dzina la Chauta ndi kulitemberera. Tsono adabwera naye kwa Mose. Dzina la mai wake linali Selomiti, mwana wa Dibiri, wa fuko la Dani. Adamuika m'ndende mpaka atadziŵa kufuna kwa Chauta. Chauta adauza Mose kuti, “Umtulutse kuzithandoko munthu wotembererayo. Onse amene adamumva akutemberera asanjike manja ao pamutu pake, kutsimikiza kuti ndi wochimwadi, ndipo mpingo wonse umponye miyala. Tsono uza Aisraele kuti, ‘Aliyense wotemberera Mulungu wake alangidwe, wonyoza dzina la Chauta ayenera kuphedwa. Mpingo wonse umponye miyala. Mlendo kapena mbadwa akangonyoza dzina la Chauta, ayenera kuphedwa. Munthu wopha mnzake ayenera kuphedwa. Munthu wopha choŵeta cha mnzake amlipire china, moyo ulipe moyo. Munthu akapundula mnzake, nayenso amchite zomwezo. Kuphwanya fupa kulipe kuphwanya fupa, diso lilipe diso, dzino lilipe dzino. Monga momwe munthu adapundulira mnzake, nayenso amchite zomwezo. Munthu wopha choŵeta cha mnzake, alipire china, koma munthu wopha mnzake ayenera kuphedwa. Lamulo la mlendo ndi mbadwa likhale limodzi lomwelo. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.’ ” Mose adauza Aisraele zimenezi, ndipo iwo adatulutsa munthu wotemberera uja m'zithandomo, namponya miyala. Motero Aisraele adachita zimene Chauta adalamula Mose. Chauta adauza Mose pa phiri la Sinai kuti, “Uza Aisraele kuti: Mukadzaloŵa m'dziko limene ndikukupatsanilo, nthaka yomwe izikapatulira Chauta chaka chasabata. Pa zaka zisanu ndi chimodzi muzikalima minda yanu, ndipo muzikathenera mitengo yanu yamphesa ndi kuthyola zipatso zake. Koma chaka chachisanu ndi chiŵiri chikhale chaka chopumuza nthaka, chaka chopatulikira Chauta, ndipo musalime minda yanu kapena kuthenera mitengo yanu yamphesa. Musakolole zimene zidamera zokha m'munda mwanu, ndipo musathyole mphesa za mitengo yanu yosathenera. Chaka chimenechi chikhale chopumuza nthaka. Chaka chachisanu ndi chiŵiri chopumulacho chidzakupatsani chakudya chokwanira nonsenu, inuyo ndi akapolo anu aamuna ndi aakazi, antchito anu pamodzi ndi alendo amene akukhala nanu. Ng'ombe zanu ndi nyama za m'dziko mwanu zizidzadya zimene nthaka idzabereka.” “Muziŵerenga masabata asanu ndi aŵiri a zaka, zaka zisanu ndi ziŵiri kuchulukitsa kasanunkaŵiri, kuti nyengo ya masabata asanu ndi aŵiri a zakayo ikwanire zaka 49 pamodzi. Tsono pa tsiku lakhumi la mwezi wachisanu ndi chiŵiri, mulize lipenga mokweza. Tsiku lochita mwambo wopepesera machimo, ndilo tsiku limene mulize lipengalo m'dziko lanu lonse. Mupatule chaka cha 50, ndipo mulengeze kuti pakhale ufulu m'dziko lonselo kwa onse amene ali m'menemo. Kwa inu chaka chimenecho chidzakhale chokondwerera zaka 50, pamene aliyense adzayenera kubwerera pa mtunda wake, ndipo aliyense mwa inu abwerere ku banja lake. Chaka chimenecho cha 50 chikhale chaka chachikondwererodi. Pa chaka chimenechi musabzale kanthu, kapena kukolola mphulumukwa, kapenanso kuthyola mphesa pa mitengo yosathenera. Chimenechi ndi chaka chokondwerera zaka 50. Chikhale chaka chopatulika kwa inu ndipo mudye zam'likale. “Chaka chimenechi chokondwerera zaka 50, aliyense abwerere pa mtunda wake. Ukagulitsa mnzako munda, kapena ukagula munda kwa mnzako, pasakhale kuchenjeretsana. Ugule kwa mnzako potsata chiŵerengero cha zaka zimene zidapita kuyambira pa chikondwerero cha chaka cha 50 chapita. Ndipo mnzakoyo akugulitse potsata chiŵerengero cha zaka zokolola zimene zatsala. Zaka zikachuluka uwonjezere mtengo, zaka zikachepa uchepetse mtengo, poti akukugulitsani potsata chiŵerengero cha zaka zokolola. Musachenjeretsane, koma muwope Mulungu wanu. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.” “Muzimvera malamulo anga ndi kutsata zimene ndikukulamulani, ndipo muzizichitadi. Potero mudzakhala m'dzikomo popanda chokuvutani. Nthaka idzakupatsani zipatso zake, mudzazidya mpaka kukhuta, ndipo mudzakhala m'dzikomo popanda chokuvutani. Mukafunsa kuti: Kodi pa chaka chachisanu ndi chiŵiri tidzadya chiyani, tikapanda kubzala kapena kukolola dzinthu? Ine ndidzalamula kuti mukhale ndi madalitso pa chaka chachisanu ndi chimodzi, kuti nthaka ibale zakudya zokwanira zaka zitatu. Pamene mubzala pa chaka chachisanu ndi chitatu muzidzadya sundwe. Mpaka chaka chachisanu ndi chinai pokolola, mudzidzadyabe sundwe.” “Mtunda usagulitsidwe mpaka muyaya, pakuti dzikolo ndi langa. Inu ndinu alendo ndiponso oyendayenda okhala ndi Ine. M'dziko monse m'mene mudzakhalemo, mudzaloleza anzanu kuwombola mtunda umene unali wao kale. “Mbale wanu akakhala wosauka, nagulitsako gawo lina la mtunda wake, wachibale wake abwere kudzaombola mtunda umene mbale wake wagulitsawo. Munthu akakhala wopanda mbale woti aombole mtundawo, ndipo pambuyo pake munthuyo nkusanduka wolemera, napeza zokwanira kuti auwombole, aŵerenge zaka kuyambira pamene adagulitsa mtundawo. Amubwezere amene adaagulayo ndalama zimene akadayenera kuzipereka mpaka chaka chokondwerera zaka 50. Atatero, atenge mtunda wake. Koma akapanda kukhala nazo zokwanira zoti aombolere, mtundawo udzakhalebe m'manja mwa amene adagulayo, mpaka pa chaka chokondwerera zaka 50. Pa chaka chimenecho mtundawo udzakhala woombola ndipo ubwerere kwa mwiniwake. “Munthu akagulitsa nyumba ya mu mzinda wozingidwa ndi linga, angathe kuiwombola chisanathe chaka chathunthu ataigulitsa. Adzatha kuiwombola pa nthaŵi yomweyo. Nyumbayo ikapanda kuwomboledwa chisanathe chaka chimodzicho, nyumba ya mu mzinda wozingidwa ndi malingawo idzakhala ya munthu amene adagulayo pa mibadwo yake yonse. Sidzaomboledwa pa chaka chokondwerera zaka 50. Koma nyumba zam'midzi, zosazingidwa ndi malinga, achite nazo monga momwe amachitira ndi minda yam'dzikomo. Angathe kuziwombola, ndipo zibwezedwe pa chaka chokondwerera zaka 50. Koma kunena za mizinda ya Alevi nyumba zimene zili m'mizinda mwao, Aleviwo angathe kuziwombola nthaŵi iliyonse. Mlevi wina akapanda kuwombola nyumba imene idagulitsidwa mumzinda mwaomoyo aibweze pa chaka chokondwerera zaka 50. Pakuti nyumba zimene zili m'mizinda ya Alevi ndi zao za Aleviwo pakati pa Aisraele. Koma minda ya m'milaga ya mizindayo singagulitsidwe, pakuti mindayo ndi yao mpaka muyaya.” “Mbale wako akakhala wosauka, ndipo sangathe kudzisamala, iweyo umthandize. Uzikhala naye monga ngati mlendo, ndiponso monga ngati munthu wokhala nao kanthaŵi. Usalandire chiwongoladzanja pa ndalama zimene adakongola, kapena kuwonjezerapo zina, koma uziwopa Mulungu wako, ndipo ulole mbale wakoyo kuti akhale nawe. Musakongoze mnzanu ndalama zanu kuti mulandire chiwongoladzanja, kapena kumpatsa chakudya kuti mupeze phindu. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu, amene ndidakutulutsani m'dziko la Ejipito kuti ndikupatseni dziko la Kanani, ndipo kuti ndikhale Mulungu wanu.” “Mbale wako amene ukukhala naye akakhala wosauka nadzigulitsa kwa iwe, usamuyese kapolo wako. Akhale ngati wantchito wako, ndiponso ngati mlendo wako. Azikugwirira ntchito mpaka chaka chokondwerera zaka 50. Pambuyo pake achoke kwa iwe, pamodzi ndi ana ake omwe, apite ku banja lake, ndi kubwerera ku choloŵa cha makolo ake. Aisraele ndi atumiki anga amene ndidaŵatulutsa ku dziko la Ejipito, asagulitsidwe ngati akapolo. Usaŵalamule mwankhalwe, koma uziwopa Mulungu wako. Kunena za akapolo aamuna kapena aakazi oti muzikhala nawo, mungathe kuŵagula kwa mitundu ina ya anthu okuzungulirani. Mungathenso kuŵagula pakati pa alendo amene akukhala pakati panu ndiponso pakati pa mabanja okhala nanu amene adabadwira m'dziko mwanu. Amenewo angathe kukhala anu. Akapolowo mungathe kuŵasiya m'manja mwa ana anu, inu mutafa, kuti akhale choloŵa chao nthaŵi zonse. Amenewo mungathe kuŵayesa akapolo, koma abale anu Aisraele musaŵalamule mwankhalwe. “Mlendo kapena munthu wodzangokhala nanu akalemera, ndipo mbale wanu wokhala naye pafupi akakhala wosauka, nadzigulitsa yekha kwa mlendoyo kapena kwa munthu wodzangokhala nanu uja, kapena kwa aliyense wa banja la mlendolo, mbale wanu wodzigulitsayo angathe kuwomboledwa. Wina mwa abale ake angathe kumuwombola, kapena mbale wa bambo wake, kapena mwana wa mbale wa bambo wake, kapena wachibale wa pabanja pake, onseŵa angathe kumuwombola. Koma wodzigulitsayo akalemera, angathe kudziwombola yekha. Aŵerengerane ndi munthu adamgulayo kuyambira chaka chimene adadzigulitsa kwa iyeyo mpaka chaka chokondwerera zaka 50. Mtengo wa kuwomboledwa kwake ukhale wolingana ndi chiŵerengero cha zakazo. Nthaŵi imene anali ndi mbuyakeyo iŵerengedwe monga ngati nthaŵi ya munthu wantchito. Zaka zikakhala kuti zikadalipo zambiri, pa mtengo umene adalipira pomgula, iye abweze mtengo womuwombolerawo. Zikangotsala zaka zoŵerengeka kuti chifike chaka chokondwerera zaka 50, aŵerengerane ndi mbuye wake, ndipo potsata zaka zotsala mpaka cha 50, abweze ndalama za kuwomboledwa kwake. Azikhala naye ngati wantchito wolembedwa, chaka ndi chaka. Asamlamule mwankhalwe, iwe ukupenya. Akapanda kuwomboledwa mwa njira zimenezi, adzaomboledwa pa chaka chokondwerera zaka 50, iyeyo pamodzi ndi ana ake. Ndithudi kwa Ine Aisraele ndi atumiki anga amene ndidaŵatulutsa m'dziko la Ejipito. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.” “Musadzipangire mafano ndipo musaimike zithunzi zosema kapena miyala yachipembedzo. Musaimiritse miyala yosema mwachithunzi m'dziko mwanu kuti muziipembedza. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu. Muzisunga masiku anga a Sabata ndi kulemekeza malo anga oyera. Ine ndine Chauta. “Mukamayenda motsata njira zanga ndi kumamvera malamulo anga onse ndi kuŵatsatadi, ndidzakupatsani mvula pa nyengo yake, ndipo nthaka idzakubalirani zokolola zochuluka, ndipo mitengo yam'minda idzakubalirani zipatso. Mudzakhala mukupuntha dzinthu mpaka nthaŵi yothyola zipatso, ndipo mudzakhala mukuthyola zipatso mpaka nthaŵi yobzala. Mudzadya chakudya mpaka kukhuta, ndi kumakhala m'dziko mwanu popanda chokuvutani. Ndidzabweretsa mtendere m'dziko mwanu, ndipo muzidzagona pansi popanda wokuwopsani. Ndidzapirikitsa zilombo zoopsa m'dziko mwanu, ndipo m'dziko mwanu simudzakhala nkhondo. Mudzapirikitsanso adani anu, ndipo mudzaŵagonjetsa ndi lupanga. Anthu asanu okha mwa inu adzapirikitsa anthu zana ndipo anthu zana mwa inu adzapirikitsa anthu zikwi khumi, ndipo adani anuwo mudzaŵagonjetsa ndi lupanga Ndidzakukumbukirani, ndipo ndidzakubalitsani ana ambiri ndi kukuchulukitsani. Ndidzalimbitsa chipangano changa ndi inu. Muzidzadyabe sundwe wakalekale, koma mudzachotsa sundweyo m'khokwe, kuti zatsopano zipeze malo. Ndidzakhala pakati panu ndipo sindidzaipidwa nanu. Ndidzayenda pakati panu. Ine ndidzakhala Mulungu wanu, inu mudzakhala anthu anga. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu, amene ndidakutulutsani ku dziko la Ejipito, kuti musakhale akapolo a Aejipito. Ndadula goli lanu kuti muziyenda moongoka. “Koma mukapanda kundimvera ndi kutsata malamulo anga onseŵa, mukamanyoza malamulo anga, ndipo mtima wanu ukamadana ndi zimene ndikulamulani, mpaka kusamvera malamulo anga onse ndi kuswa chipangano changa, ndidzakuchitani izi: ndidzabweretsa zoopsa zadzidzidzi, chifuwa chachikulu choondetsa ndiponso malungo oononga maso ndi ofooketsa moyo. Mudzabzala mbeu zanu, koma osakololapo kanthu, chifukwa choti adani anu adzazidya. Ndidzakufulatirani, ndipo adani anu adzakugonjetsani. Odana nanu adzakulamulani, ndipo muzidzangothaŵa popanda wokupirikitsani. Mukapanda kundimvera mutaona zonsezi, ndidzakulanganinso mochulukitsa kasanunkaŵiri chifukwa cha machimo anu. Ndidzaononga nyonga zanu zimene mukunyadirazo, ndipo ndidzasandutsa mitambo kuti ikhale youma ngati chitsulo, ndiponso nthaka yanu kuti ikhale ngati mkuŵa. Nyonga zanu zidzapita pachabe, poti nthaka yanu sidzabala kanthu, ndipo mitengo yake sidzabala zipatso. “Tsono mukamayenda motsutsana ndi Ine osandimvera, ndidzabweretsa miliri inanso pa inu, yopambana machimo anu kasanunkaŵiri. Ndidzabweretsanso zilombo zolusa pakati panu, zimene zidzakudyerani ana anu, ndi kukuwonongerani ng'ombe zanu. Zilombozo zidzachepetsa chiŵerengero chanu, kotero kuti m'njira zanu simuzidzapita anthu. “Mukapanda kubwerera kwa Ine nditakulangani chotere, ndipo mukachitabe zotsutsana ndi Ine, Inenso ndidzalimbana nanu, ndipo ndidzakulangani mochulukitsa kasanunkaŵiri chifukwa cha machimo anuwo. Ndidzabweretsa lupanga pa inu limene lidzakulangani chifukwa chophwanya chipangano changa. Ndipo mukasonkhana m'mizinda mwanu, ndidzatumiza miliri pakati panu ndipo ndidzakuperekani m'manja mwa adani anu. Ndidzachepetsa buledi wanu wa tsiku ndi tsiku mpaka akazi khumi adzapanga buledi mu uvuni umodzi. Ndipo adzakugaŵirani bulediyo pang'onopang'ono. Choncho mudzadya, koma osakhuta. “Mukapanda kundimvera mutaona zonsezi, ndipo mukachitabe zotsutsana ndi Ine, Inenso ndidzalimbana nanu mwaukali, ndipo Ine mwiniwake ndidzakulangani mochulukitsa kasanunkaŵiri chifukwa cha machimo anu. Mudzadya ana anu aamuna, ndipo mudzadyanso ana anu aakazi. Ndidzaononga akachisi anu opembedzerako mafano ku mapiri ndi kugwetsa maguwa anu ofukizirapo lubani, ndipo ndidzaponya mitembo yanu pa mafano opanda moyo, ndipo ndidzadana nanu. Ndidzasandutsa mizinda yanu kuti ikhale mabwinja, ndidzasandutsanso malo anu achipembedzo kuti akhale opanda anthu, ndipo sindidzalolanso kumva fungo lokoma la zopereka zanu. Ndidzaononga dziko lanu kotero kuti adani anu amene adzakhale m'menemo adzadabwa. Ndidzakubalalitsani pakati pa mitundu ina ya anthu ndipo ndidzakupirikitsani, lupanga lili pambuyo. Dziko lanu lidzasanduka chipululu, ndipo mizinda yanu idzasanduka mabwinja. “Pa nyengo imeneyo nthaka idzakondwerera zaka zoipumitsa nthaŵi yonse pamene m'dzikomo mulibe anthu, inu muli m'dziko la adani anu. Pamenepo nthaka idzapuma ndi kukondwerera zaka zopumazo. Nthaŵi zonse pamene dzikolo lilibe anthu, nthaka idzapuma, kupuma kwake kumene sidapumepo pa zaka zonse pamene inu munkakhalamo. Ndipo ngakhale ena amene mudzatsalenu, ndidzaika mtima wa mantha mwa inu pamene muli m'dziko la adani anu. Mtswatswa wa tsamba louluka udzakuthaŵitsani. Mudzathaŵa monga m'mene munthu amathaŵira lupanga, ndipo mudzagwa pansi popanda okuthamangitsani. Mudzaphunthwitsana monga ngati mukuthaŵa nkhondo, ngakhale palibe amene akukupirikitsani. Ndipo simudzakhala ndi mphamvu zoti mulimbane ndi adani anu. Mudzatha, kuchita kuti psiti, pakati pa mitundu ya anthu, ndipo dziko la adani anu lidzakudyani. Ngakhale ena amene mudzatsalenu, nanunso mudzazunzika m'dziko la adani anu chifukwa cha machimo anu, ndipo mudzazunzikanso chifukwa cha machimo a makolo anu. “Tsono adzaulula machimo ao ndi machimo a makolo ao chifukwa cha kunyenga kwao kumene adandinyenga nako, ndiponso chifukwa cha kuyenda motsutsana ndi Ine. Paja chifukwa cha zimenezo Ine ndidatsutsana nawo ndi kuŵafikitsa ku dziko la adani ao. Tsono mitima yao youma idzadzichepetsa ndi kulola kulangidwa chifukwa cha machimo ao. Pamenepo ndidzakumbukira chipangano changa ndi Yakobe, Isaki, ndi Abrahamu, ndipo dzikolo ndidzalikumbukira. Koma ayambe aisiya nthaka yaoyo, kuti ikondwerere zaka zoipumuza, pamene dziko lili lopanda anthu, iwo atachoka. Tsono iwo adzalangika chifukwa cha machimo ao, popeza kuti adanyoza zimene ndidaŵalamula, ndipo mitima yao idadana ndi malangizo anga. Ngakhale zitachitika zonsezo, pamene ali m'dziko la adani ao, sindidzaŵanyoza ndipo sindidzadana nawo mpaka kuŵaononga kwathunthu ndi kuphwanya chipangano changa ndi iwo, chifukwa Ine ndine Chauta, Mulungu wao. Koma poŵachitira chifundo ndidzakumbukira chipangano changa ndi makolo ao amene ndidaŵatulutsa ku dziko la Ejipito, mitundu ina ya anthu ikupenya, kuti ndikhale Mulungu wao. Ine ndine Chauta.” Ameneŵa ndiwo malamulo ndi malangizo amene Chauta adaika pakati pa Iye mwini ndi Aisraele pa phiri la Sinai, kudzera mwa Mose. Chauta adauza Mose kuti, “Uza Aisraele kuti: Ngati munthu adalumbira kuti adzapereka munthu mnzake kwa Mulungu, koma pambuyo pake akufuna kumuwombola, zoyenera kupereka ndi izi: pa munthu wamwamuna wa zaka makumi aŵiri mpaka zaka 60, pakhale masekeli asiliva 50, potsata kaŵerengedwe ka kunyumba ya Mulungu. Munthu wake akakhala wamkazi, mtengo wake ukhale wokwana masekeli asiliva makumi atatu. Akakhala munthu wa zaka zisanu mpaka zaka makumi aŵiri, mtengo wake ukhale wokwana masekeli asiliva makumi aŵiri pa munthu wamwamuna, ndipo khumi pa munthu wamkazi. Akakhala munthu wa mwezi umodzi mpaka zaka zisanu, mtengo wake ukhale wokwana mashekeli asiliva zisanu pa munthu wamwamuna, ndipo zitatu pa munthu wamkazi. Munthu wake akakhala wa zaka 60 kapena kupitirirapo, mtengo wake ukhale wokwana masekeli asiliva 15 pa munthu wamwamuna, ndipo khumi pa munthu wamkazi. Munthu akakhala wosauka kwambiri kuti sangathe kulipira mtengo umenewo, abwere ndi munthu woperekedwa uja kwa wansembe, ndipo wansembeyo aike mtengo pa iye. Mtengo umene wansembeyo aike ukhale wolingana ndi momwe munthu wolumbirayo angalipire. “Ikakhala nyama yonga imene anthu amaperekera nsembe kwa Chauta, zonse zimene anthu amapereka kwa Chauta nzopatulika. Munthu asapereke ina m'malo mwake kapena kuisinthitsa ndi ina, asapereke yabwino m'malo mwa yoipa, kapena yoipa m'malo mwa yabwino. Ndipo akasinthitsa nyama ina ndi inzake, nyamayo pamodzi ndi inzake waisinthitsayo zikhala zopatulika. Ikakhala nyama yonyansa, yonga imene siloledwa kuipereka ngati nsembe kwa Chauta, munthuyo abwere ndi nyamayo kwa wansembe. Ndipo wansembe atchule mtengo wake poona ngati njabwino kapena ai. Monga momwe iwe wansembe utchulire, mtengo udzakhala momwemo. Koma akafuna kuti aiwombole, aonjezepo pa mtengo wake wa nyamayo chimodzi mwa zigawo zisanu za mtengo wakewo. “Pamene munthu apereka nyumba yake kuti ikhale yopatulikira Chauta, wansembe aiwone ngati ili yabwino kapena ai. Monga momwe wansembe aiwonere, idzakhala momwemo. Munthu woiperekayo akafuna kuti aombole nyumba yakeyo, pa mtengo wake wa nyumbayo aonjezepo chimodzi mwa zigawo zisanu za mtengowo, ndipo idzakhala yake. “Munthu akapereka kwa Chauta chigawo cha dera la choloŵa chake, mtengo umene uike ukhale wolingana ndi mbeu zodzabzalamo. Pa mbeu za barele zokwanira makilogaramu 20, mtengo wake ukhale wokwana mashekeli asiliva 50. Akapereka munda wake kuyambira pa chaka chokondwerera zaka 50, mtengo wake ukhale wathunthu monga momwe iwe udaikira. Koma akapereka munda wake chitatha chaka chokondwerera zaka 50, wansembe aŵerenge mtengo wa ndalama molingana ndi zaka zotsala kuti chifike chaka china chokondwerera zaka 50, ndipo achotse pa mtengo umene wansembe waika. Munthu amene adapereka munda, akafuna kuti auwombole, pa mtengo wa mundawo aonjezepo chimodzi mwa zigawo zisanu za mtengowo, ndipo udzakhala wake. Koma ngati safuna kuti aombole kapena ngati waugulitsa kwa munthu wina, mundawo sudzaombolekanso. Mwini mundawo atausiya pa chaka chokondwerera zaka 50, udzakhala wopatulikira Chauta ngati munda woperekedwa. Wansembe adzautenga kuti ukhale wake. Munthu akapereka kwa Chauta munda umene waugula, umene suli chigawo cha choloŵa chake, wansembe aŵerenge mtengo wake kufikira pa chaka chokondwerera zaka 50. Tsono munthuyo apereke ndalama zokwanira mtengo wake pa tsikulo, kuti zikhale zopatulikira Chauta. Pa chaka chokondwerera zaka 50, mundawo udzabwezedwa kwa munthu amene adaugulitsayo, amene mtundawo unali wake ngati choloŵa chake. Potchula mtengo uliwonse, wansembe aziŵerenga monga momwe amaŵerengera m'Nyumba ya Chauta, ndiye kuti sekeli imodzi ikwanire magera makumi aŵiri. “Koma pasakhale munthu amene apereke mwana woyamba wa nyama. Mwanayo ali kale wa Chauta, popeza kuti ndi woyamba. Ngakhale ikhale ng'ombe kapena nkhosa, nja Chauta imeneyo. Ikakhala nyama yonyansa pa chipembedzo, aiwombole pa mtengo umene wansembe aike, ndipo aonjezepo chimodzi mwa zigawo zisanu za mtengo wake. Koma akapanda kuiwombola, igulitsidwe pa mtengo umene wansembe aike. “Koma chinthu chilichonse choperekedwa kwathunthu kwa Chauta, kaya ndi munthu kapena nyama kapena munda umene uli choloŵa chake, chisagulitsidwe kapena kuwomboledwa. Chinthu chilichonse choperekedwa choncho kwa Chauta, nchopatulika kopambana. Munthu aliyense amene waperekedwa kotheratu, sangathe kuwomboledwa, aziphedwa basi. “Chigawo chilichonse chachikhumi cham'dziko, kaya ndi cha mbeu zam'nthaka, kaya ndi cha zipatso zam'mitengo, nchake cha Chauta. Chimenecho nchopatulikira Chauta. Munthu akafuna kuti aombole chigawo chimodzi chachikhumi chilichonse, aonjezepo chimodzi mwa zigawo zisanu za mtengo wake. Ndipo chigawo chachikhumi chilichonse cha nsambi wa ng'ombe ndi wa nkhosa, ndiye kuti nyama yachikhumi iliyonse imene mbusa aiŵerenge, ikhale yopatulikira Chauta. Mwiniwake asafunse ngati nyamayo njabwino kapena njoipa, ndipo asaisinthitse. Akaisinthitsa ndi ina, imeneyo pamodzi ndi imene waisinthitsayo zidzakhala zopatulikira Chauta, ndipo sangaziwombole.” Ameneŵa ndiwo malamulo amene Chauta adalamula Mose pa phiri la Sinai kuti auze Aisraele. Chauta adalankhula ndi Mose ku chipululu cha Sinai, m'chihema chamsonkhano, pa tsiku loyamba la mwezi wachiŵiri, chaka chachiŵiri atatuluka ku dziko la Ejipito, ndipo adamuuza kuti, “Uŵerenge anthu a mpingo wonse wa Aisraele potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Ulembe dzina la munthu wamwamuna aliyense mmodzimmodzi. Iwe ndi Aroni muŵerenge anthu, gulu ndi gulu, a zaka makumi aŵiri ndi opitirirapo, ndiye kuti anthu onse a ku Israele amene angathe kumenya nkhondo. Pa fuko lililonse mutenge munthu mmodzi, mtsogoleri wa banja lake, kuti akuthandizeni pa ntchito yanuyo. Maina a anthu okuthandizaniwo ndi aŵa: fuko la Rubeni, akuthandizeni ndi Elizuri mwana wa Sedeuri; fuko la Simeoni, Selumiele mwana wa Zurishadai; fuko la Yuda, Nasoni mwana wa Aminadabu; fuko la Isakara, Netanele mwana wa Zuwara; fuko la Zebuloni, Eliyabu mwana wa Heloni. Mwa ana a Yosefe: fuko la Efuremu, Elisama mwana wa Amihudi; fuko la Manase, Gamaliele mwana wa Pedazuri; fuko la Benjamini, Abidani mwana wa Gideoni; fuko la Dani, Ahiyezere mwana wa Amishadai; fuko la Asere, Pagiyele mwana wa Okarani; fuko la Gadi, Eliyasafu mwana wa Deuwele; fuko la Nafutali, Ahira mwana wa Enani.” Ameneŵa ndiwo anthu amene adasankhidwa mu mpingo, atsogoleri a mabanja ao, akulu a mafuko a Aisraele. Mose ndi Aroni adaŵatenga anthu amene atchulidwaŵa, ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wachiŵiri, adasonkhanitsa mpingo wonse. Tsono Aisraele adalembetsa maina ao potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Ankalembetsa ndi anthu a zaka makumi aŵiri ndi kupitirirapo, mmodzimmodzi, monga momwe Chauta adaalamulira Mose. Umu ndi m'mene adaŵerengera anthuwo m'chipululu cha Sinai. Mwa zidzukulu za Rubeni, mwana woyamba wa Yakobe, adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Rubeni, adapezeka kuti ali 46,500. Mwa zidzukulu za Simeoni adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Simeoni, adapezeka kuti ali 59,300. Mwa zidzukulu za Gadi adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Gadi, adapezeka kuti ali 45,650. Mwa zidzukulu za Yuda adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Yuda, adapezeka kuti ali 74,600. Mwa zidzukulu za Isakara adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Isakara, adapezeka kuti ali 54,400. Mwa zidzukulu za Zebuloni adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Zebuloni, adapezeka kuti ali 57,400. Mwa zidzukulu za Yosefe, ndiye kuti anthu a m'fuko la Efuremu, adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Efuremu, adapezeka kuti ali 40,500. Mwa zidzukulu za Manase adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Manase, adapezeka kuti ali 32,200. Mwa zidzukulu za Benjamini adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Benjamini, adapezeka kuti ali 35,400. Mwa zidzukulu za Dani adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Dani, adapezeka kuti ali 62,700. Mwa zidzukulu za Asere adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Asere, adapezeka kuti ali 41,500. Mwa zidzukulu za Nafutali adalemba maina a amuna onse otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Nafutali, adapezeka kuti ali 53,400. Ameneŵa ndiwo anthu amene Mose ndi Aroni adaŵaŵerenga, mothandizidwa ndi atsogoleri a Aisraele khumi ndi aŵiri amene ankaimirira mafuko ao. Choncho amuna onse a mu Israele otha kumenya nkhondo, a zaka 20 ndi a zaka zopitirirapo, potsata banja la makolo ao, adapezeka kuti ali 603,550. Alevi okha sadaŵaŵerengere kumodzi ndi enawo, potsata banja la makolo ao, chifukwa Chauta adaauza Mose kuti, “Fuko la Levi usaliŵerenge ai, anthu ake usaŵalembere kumodzi ndi Aisraele enawo. Uike Aleviwo kuti aziyang'anira chihema changa chaumboni, zipangizo zake ndi zonse zimene zili m'menemo. Azinyamula chihemacho, pamodzi ndi zipangizo zake, ndipo azichisamala. Zithando zao azimange pozungulira chihemacho. Nthaŵi imene anthu akunyamuka ulendo, Alevi ndiwo amene azichitsitsa, ndipo nthaŵi imene anthu aima, Alevi omwewo ndiwo amene azichiimiritsa. Munthu wina aliyense wochiyandikira adzaphedwa. Aisraele azimanga mahema ao m'magulumagulu, aliyense pa chithando chake, ndipo onse azimanga pafupi ndi mbendera yao. Koma Alevi amange mahema ao pozungulira chihema chaumboni, kuti Mulungu asakwiyire mpingo wa Aisraele. Alevi ndiwo amene aziyang'anira chihema chaumbonicho.” Umu ndi m'mene adachitira Aisraele. Adachita zonse monga momwe Chauta adaalamulira Mose. Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti, “Aisraele, pomanga zithando, aliyense azimanga pafupi ndi mbendera yake imene ili ndi zizindikiro za banja la kholo lake. Azimanga moyang'anana ndi chihema chamsonkhano, tsono mochizungulira. Amene amange kuvuma, kotulukira dzuŵa, akhale a mbendera ya zithando za fuko la Yuda, m'magulumagulu. Mtsogoleri wa fuko la Yudalo ndi Nasoni, mwana wa Aminadabu, ndipo ankhondo ake ngokwanira 74,600. Amene amange pafupi ndi fuko lake akhale a fuko la Isakara. Mtsogoleri wa fuko la Isakaralo ndi Netanele mwana wa Zuwara, ndipo ankhondo ake ngokwanira 54,400. Tsono pabwere fuko la Zebuloni, limene mtsogoleri wake ndi Eliyabu mwana wa Heloni, ndipo ankhondo ake ngokwanira 57,400. Gulu lonse lathunthu la ku zithando za Yuda, poŵerenga magulu atatu onseŵa, ndi 186,400. Iwowo azikhala patsogolo poyenda. “Mbali yakumwera kuzikhala mbendera ya zithando za fuko la Rubeni, m'magulumagulu. Mtsogoleri wa fuko la Rubeni ndi Elizuri mwana wa Sedeuri, ndipo ankhondo ake ngokwanira 45,500. Amene amange pafupi ndi fuko lake akhale a fuko la Simeoni, limene mtsogoleri wake ndi Selumiele mwana wa Zurishadai, ndipo ankhondo ake ngokwanira 59,300. Tsono pabwere fuko la Gadi, limene mtsogoleri wake ndi Eliyasafu, mwana wa Deuwele, ndipo ankhondo ake ngokwanira 45,650. Chiŵerengero chathunthu cha anthu a m'zithando za Rubeni, poŵerenga magulu atatu onseŵa, ndi 151,450. Iwo akhale a gulu lachiŵiri poyenda. “Pamenepo mpamene anyamule chihema chamsonkhano, chifukwa zithando za Alevi zimakhala pakati pa zithando zina. Monga momwe adamangira zithando zao, ndimo aziyendera, gulu lililonse pamalo pake motsatira mbendera yake. “Mbali yakuzambwe kuzikhala mbendera ya zithando za fuko la Efuremu, m'magulumagulu. Mtsogoleri wa fuko la Efuremulo ndi Elisama mwana wa Amihudi, ndipo ankhondo ake ngokwanira 40,500. Amene amange pafupi ndi fuko lake akhale a fuko la Manase, limene mtsogoleri wake ndi Gamaliele mwana wa Pedazuri, ndipo ankhondo ake ngokwanira 32,200. Tsono pabwere fuko la Benjamini, limene mtsogoleri wake ndi Abidani mwana wa Gideoni, ndipo ankhondo ake ngokwanira 35,400. Chiŵerengero chathunthu cha anthu a m'zithando za Efuremu, poŵerenga magulu atatu onseŵa, ndi 108,100. Iwo akhale a gulu lachitatu poyenda. “Mbali yakumpoto kuzikhala mbendera ya zithando za fuko la Dani, m'magulumagulu. Mtsogoleri wa fuko la Danilo ndi Ahiyezere mwana wa Amishadai, ndipo ankhondo ake ngokwanira 62,700. Amene amange pafupi ndi fuko lake akhale a fuko la Asere, limene mtsogoleri wake ndi Pagiyele mwana wa Okarani, ndipo ankhondo ake ngokwanira 41,500. Tsono pabwere fuko la Nafutali, limene mtsogoleri wake ndi Ahira mwana wa Enani, ndipo ankhondo ake ngokwanira 53,400. Chiŵerengero chathunthu cha anthu a m'zithando za Dani ndi 157,600. Iwo akhale a gulu lotsiriza poyenda motsatira mbendera zao.” Ameneŵa ndiwo Aisraele monga momwe adaŵaŵerengera potsata banja la makolo ao. Anthu onse a m'zithandomo anali 603,550 amene adaŵaŵerenga m'magulumagulu. Koma Alevi sadaŵaŵerengere kumodzi ndi Aisraele, monga momwe Chauta adaalamulira Mose. Umu ndi m'mene adachitira Aisraele. Iwo adachita zonse monga momwe Chauta adaalamulira Mose. Adamanga zithando zao pafupi ndi mbendera zao. Choncho adanyamuka ulendo wao aliyense pa banja lake, potsata banja la makolo ao. Nayi mibadwo ya Aroni ndi Mose pa nthaŵi imene Chauta adalankhula ndi Mose pa phiri la Sinai. Maina a ana a Aroni naŵa: Nadabu mwana wake wachisamba, Abihu, Eleazara ndi Itamara. Ameneŵa ndiwo maina a ana a Aroni, ansembe odzozedwa amene iye adaŵasankha kuti azitumikira pa ntchito yaunsembe. Koma Nadabu ndi Abihu adafa pamaso pa Chauta pamene adapereka moto wosaloledwa pamaso pa Chauta m'chipululu cha Sinai. Iwowo analibe ana, ndipo choncho Eleazara ndi Itamara adatumikira pa ntchito yaunsembe pa nthaŵi imene Aroni bambo wao anali moyo. Chauta adauza Mose kuti, “Bwera nawo anthu a fuko la Levi, ndipo uŵapereke kwa wansembe Aroni kuti azimtumikira. Azigwirira ntchito iyeyo ndi mpingo wonse, pakhomo pa chihema chamsonkhano, monga momwe amachitira potumikira m'Chihema cha Mulungu. Aziyang'anira zipangizo zonse za m'chihema chamsonkhano, ndipo azigwirira Aisraele ntchito potumikira m'Chihema cha Mulungu. Aleviwo uŵapereke kwa Aroni ndi kwa ana ake aamuna. Uŵapereke kwathunthu kwa iyeyo, kuŵachotsa pakati pa Aisraele. Umusankhe Aroni ndi ana ake, kuti azitumikira pa ntchito yaunsembe. Koma wina aliyense akayandikira pafupi, aphedwe.” Chauta adauza Mose kuti, “Pakati pa Aisraele, ndaŵapatula Alevi, m'malo mwa mwana wamwamuna aliyense woyamba kubadwa, amene amatsekula mimba ya mai wake. Aleviwo ndi anga, pakuti ana onse aamuna oyamba kubadwa ndi anga. Pa tsiku lija lomwe ndidapha ana onse aamuna oyamba kubadwa m'dziko la Ejipito, ndidadzipatulira ana onse oyamba kubadwa a m'dziko la Israele, ana a anthu ndi a nyama omwe. Onsewo ndi anga, Ine ndine Chauta.” Chauta adauza Mose m'chipululu cha Sinai kuti, “Uŵerenge ana aamuna a Levi potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Uŵerenge wamwamuna aliyense kuyambira wa mwezi umodzi ndi wopitirirapo.” Choncho Mose adaŵaŵerenga potsata mau a Chauta monga momwe adamlamulira. Maina a ana a Leviwo ndi aŵa: Geresoni, Kohati ndi Merari. Tsono ana a Geresoni potsata mabanja ao naŵa: Labini ndi Simei. Ana a Kohati potsata mabanja ao ndi aŵa: Amuramu, Izara, Hebroni ndi Uziyele. Ndipo ana a Merari potsata mabanja ao ndi aŵa: Mali ndi Musi. Ameneŵa ndiwo mabanja a Levi potsata banja la makolo ao. Alibini ndi Asimei anali mabanja otuluka mwa Geresoni. Ameneŵa ndiwo anali mabanja a Ageresoni. Chiŵerengero chao potsata kuchuluka kwa amuna onse, kuyambira mwana wamwamuna wa mwezi umodzi ndi wopitirapo, chinali 7,500. Mabanja a Geresoni ankamanga zithando zao kumbuyo kwa chihema cha Mulungu mbali yakuzambwe. Eliyasafu mwana wa Laele ndiye anali mtsogoleri wa banja la makolo a Ageresoni. Ndipo ntchito imene ana a Geresoni adapatsidwa m'chihema chamsonkhano inali yosamala chihema cha Mulungu, pamodzi ndi chophimbira chake, nsalu yochinga pakhomo pa chihema chamsonkhano, nsalu zochingira bwalo, nsalu zochingira khomo la bwalo lozungulira chihema cha Mulungu ndi guwa lansembe, ndiponso zingwe zake. Ankagwira ntchito zonse zokhudza zimenezi. Aamuramu, Aizari, Ahebroni ndi Auziyele, anali mabanja otuluka mwa Kohati. Ameneŵa ndiwo amene anali mabanja a Akohati. Potsata chiŵerengero cha amuna onse kuyambira mwana wamwamuna wa mwezi umodzi ndi wopitirirapo, onse anali 8,600, amene ankagwira ntchito m'malo opatulika. Mabanja a ana a Kohati ankamanga zithando zao kumwera kwa chihema cha Mulungu, pamodzi ndi Elizafani, mwana wa Uziyele, amene anali mutu wa mabanja a Akohati, Ndipo ntchito imene iwo adapatsidwa inali yosamala Bokosi lachipangano, tebulo, choikaponyale, maguwa, zipangizo za m'malo opatulika zimene ansembe ankagwirira ntchito, pamodzi ndi nsalu yochingira. Ankagwira ntchito zonse zokhudza zimenezi. Tsono Eleazara mwana wa wansembe Aroni, ndiye amene anali mkulu wa atsogoleri a Alevi, ndiponso amene ankayang'anira iwo amene ankasamala malo opatulika. Amali ndi Amusi anali mabanja otuluka mwa Merari. Ameneŵa ndiwo amene anali mabanja a Merari. Chiŵerengero chao potsata kuchuluka kwa amuna onse, kuyambira mwana wamwamuna wa mwezi umodzi ndi wopitirirapo, chinali 6,200. Ndipo munthu amene anali mutu wa mabanja a Merari anali Zuriyele mwana wa Abihaili. Iwo ankamanga zithando zao kumpoto kwa chihema cha Mulungu. Ntchito imene ana aamuna a Merari adapatsidwa, inali yosamala mitengo ya malo opatulika monga: nsichi zake, mizati yake, masinde ake ndi zina zonse zoyendera limodzi ndi zimenezo. Ankayang'anira ntchito zonse zokhudza zimenezi. Ankasamalanso mizati yozungulira bwalo ndi masinde ake, ndiponso zikhomo zake ndi zingwe zake. Amene ankamanga zithando zao patsogolo pa chihema cha Mulungu kuvuma kotulukira dzuŵa, kutsogolo kwa chihema chamsonkhano, anali Mose ndi Aroni pamodzi ndi ana ake a Aroni. Iwoŵa adaŵapatsa udindo wosamala kayendetsedwe ka chipembedzo m'malo opatulika, zonse zimene ankayenera kuchita m'malo mwa Aisraele. Munthu wina aliyense wofika pafupi ankayenera kuphedwa. Alevi onse amene Mose pamodzi ndi Aroni adaŵerenga potsata mabanja ao, Chauta ataŵalamula kutero, ndiye kuti amuna onse kuyambira a mwezi umodzi ndi opitirirapo, anali 22,000. Chauta adauza Mose kuti, “Uŵerenge ana achisamba onse aamuna a Aisraele, kuyambira a mwezi umodzi ndi opitirirapo, potchula maina ao. Tsono unditengere Alevi m'malo mwa ana achisamba onse pakati pa Aisraele, utengenso ng'ombe za Alevi m'malo mwa ana onse oyamba kubadwa pakati pa ng'ombe za Aisraele, Ine ndine Chauta.” Choncho Mose adaŵerenga ana onse achisamba, monga Chauta adamlamula. Ndipo ana onse achisamba aamuna, potsata chiŵerengero cha maina ao, kuyambira a mwezi umodzi ndi opitirirapo, adakwanira 22,273. Chauta adauza Mose kuti, “Utenge Alevi m'malo mwa ana onse achisamba pakati pa Aisraele, utengenso ng'ombe za Alevi m'malo mwa ng'ombe za Aisraele. Aleviwo ndi anga, Ine ndine Chauta. Pofuna kuwombola ana achisamba 273 a Aisraele amene aposa chiŵerengero cha amuna a fuko la Levi, utenge masekeli asiliva asanu pa munthu aliyense. Masekeliwo akhale olingana ndi masekeli asiliva a ku malo opatulika kumene sekeli imodzi ikwanira magera makumi aŵiri. Upatse Aroni pamodzi ndi ana ake aamuna ndalama zimenezi, kuti zikhale mtengo woombolera Aisraele a chiŵerengero chopitirira chija.” Choncho Mose adatenga ndalama zoombolera zija kwa Aisraele amene chiŵerengero chao chidapitirira chiŵerengero cha amene adaomboledwa ndi Alevi. Adatenga ndalama zasiliva kwa ana achisamba a Aisraele okwanira 1,365, molingana ndi kaŵerengedwe ka masekeli asiliva a ku Chihema cha Mulungu. Ndipo Mose adapereka ndalama zoombolerazo kwa Aroni ndi kwa ana ake, potsata mau amene Chauta adalamula Mose. Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti, Mwa ana a Levi muŵerenge ana a Kohati, potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Muŵerenge amuna kuyambira a zaka makumi atatu mpaka a zaka makumi asanu, onse amene angathe kutumikira pa ntchito ya m'chihema chamsonkhano. Ntchito imene ana a Kohati ayenera kugwira m'chihema chamsonkhanomo ndi iyi: azisamala zinthu zopatulika kopambana. Pamene anthu akusamuka pamodzi ndi mahema ao, Aroni pamodzi ndi ana ake aloŵe m'chihema chamsonkhano, amasule nsalu yochinga, ndipo aphimbire Bokosi laumboni. Pambuyo pake ayalepo zikopa zambuzi, ndipo pamwamba pake ayalepo nsalu yobiriŵira, ndi kupisa mphiko m'zigwinjiri zake. Ayale nsalu yobiriŵira pa tebulo la buledi wokhala pamenepo nthaŵi zonse, ndi kuikapo mbale zake, zipande zake zotapira lubani, mabeseni ake, ndi zikho za chopereka cha chakumwa. Aikeponso buledi wokhala pamenepo nthaŵi zonse. Tsono pamwamba pa zimenezo ayalepo nsalu yofiira, ndi kuziphimba zonsezo ndi zikopa zambuzi, ndipo apise mphiko m'zigwinjiri zake. Atenge nsalu yobiriŵira ndi kuphimba choikaponyale, pamodzi ndi nyale zake, mbaniro zake, mbale za phulusa ndi ziŵiya zake zonse za mafuta. Ndipo achiike pamodzi ndi zipangizo zake zonse m'thumba la zikopa zambuzi, ndi kuchiika pa chonyamulira chake. Ayale nsalu yobiriŵira pa guwa lagolide, ndi kuliphimba ndi zikopa zambuzi, ndipo apise mipiko m'zigwinjiri zake. Atenge zipangizo zonse zimene amagwiritsa ntchito m'malo opatulika, aziike m'nsalu yobiriŵira, ndipo aziphimbe ndi zikopa zambuzi, ndi kuziika pa chonyamulira chake. Ataye phulusa lapaguwa, ndipo ayalepo nsalu yofiira. Aikepo ziŵiya zonse zapaguwa zimene amagwiritsira ntchito pamenepo, monga zofukizira lubani, zitsulo zokoŵera nyama, zoolera phulusa ndi mabeseni, kungoti ziŵiya zonse za pa guwalo. Pa zonsezo ayalepo zikopa zambuzi, ndipo apise mipiko m'zigwinjiri zake. Tsono Aroni ndi ana ake, atamaliza kuphimba malo opatulika pamodzi ndi zipangizo zake zonse, pamene anthu akusamuka, ana a Kohati ndiwo abwere kudzanyamula zimenezi, koma asakhudze zinthu zopatulika, kuti angafe. Zimenezi ndizo zinthu za m'chihema chamsonkhano zimene ana a Kohati azinyamula. “Eleazara mwana wa wansembe Aroni, azisamala mafuta a nyale, lubani wonunkhira, chopereka cha chakudya choperekedwa nthaŵi zonse, ndi mafuta odzozera. Aziyang'anira malo opatulika ndi zonse za m'kati mwake, ndiponso chipinda chopatulika kwambiri ndi zipangizo zake.” Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti, “Musalole kuti a m'banja la Kohati aonongeke pakati pa Alevi. Kuti Akohatiwo asafe, akayandikira zinthu zopatulika kopambana, Aroni pamodzi ndi ana ake aloŵe, ndipo apatse aliyense mwa Akohatiwo zoti achite ndi zoti anyamule. Koma asaloŵe kukayang'ana zinthu zopatulika mpang'ono pomwe, kuti angafe.” Chauta adauza Mose kuti, “Uŵerengenso ana a Geresoni potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Uŵerenge amuna kuyambira a zaka makumi atatu mpaka a zaka makumi asanu, onse amene angathe kutumikira m'chihema chamsonkhano. Zimene mabanja a Geresoni ayenera kuchita, ndiponso zimene ayenera kumanyamula ndi izi: azinyamula nsalu zochinga malo opatulika, chihema chamsonkhano pamodzi ndi chophimbira chake, zikopa zambuzi zophimba pamwamba pake, ndiponso nsalu zochinga pa khomo la chihema chamsonkhano. Azinyamulanso nsalu zochingira bwalo, nsalu yochingira khomo la pa chipata cha bwalo lozungulira malo opatulika ndi guwa, zingwe zake ndi zipangizo zina zonse zofunika. Agwire ntchito zonse zimene aŵapatse. Amene aziyang'anira ntchito zonse za ana a Ageresoni, ndi Aroni pamodzi ndi ana ake. Aziyang'anira zonse zimene ayenera kunyamula, ndi zonse zimene ayenera kuchita. Ndinu amene mudzayenera kuŵafotokozera udindo wa kunyamula zonse zija. Imeneyi ndi ntchito ya mabanja a ana a Ageresoni m'chihema chamsonkhano, ndipo woyang'anira ntchitoyo akhale Itamara, mwana wa wansembe Aroni. “Uŵerenge ana a Merari potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Uŵerenge amuna kuyambira a zaka makumi atatu mpaka a zaka makumi asanu, aliyense amene angathe kutumikira m'chihema chamsonkhano. Zimene iwo alamulidwa kuti anyamule pa ntchito yao ya m'chihema chamsonkhano nazi: anyamule mitengo ya malo opatulika monga mafulemu ake, mizati yake ndi masinde ake. Anyamulenso mizati yozungulira bwalo, pamodzi ndi zikhomo zake, zingwe zake, kudzanso zipangizo zake zonse, ndi zina zonse zoyendera limodzi ndi zimenezo. Poŵauza zinthu zimene aliyense ayenera kunyamula, uzitchula chinthu chilichonse chimodzichimodzi. Imeneyi ndiyo ntchito ya mabanja a ana a Merari, ndipo ntchito yao yonse ya m'chihema chamsonkhanoyo, aziiyang'anira ndi Itamara, mwana wa wansembe Aroni.” Tsono Mose ndi Aroni, pamodzi ndi atsogoleri a mpingo, adaŵerenga ana a Akohati potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Adaŵaŵerenga anthuwo kuyambira a zaka makumi atatu mpaka a zaka makumi asanu, onse amene ankatha kutumikira m'chihema chamsonkhano, ndipo chiŵerengero chao chidakwanira 2,750 potsata mabanja ao. Chimenecho ndicho chinali chiŵerengero cha anthu a m'mabanja a Akohati, onse amene ankatumikira m'chihema chamsonkhano, amene Mose ndi Aroni adaŵaŵerenga, monga momwe Chauta adaalamulira kudzera mwa Mose. Adaŵerenganso ana a Geresoni potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao, kuyambira anthu a zaka makumi atatu mpaka makumi asanu, onse amene ankatha kutumikira m'chihema chamsonkhano. Chiŵerengero chao chidakwanira 2,630 potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Chimenechi ndicho chinali chiŵerengero cha anthu a m'banja a Ageresoni, amene ankatumikira m'chihema chamsonkhano, amene Mose ndi Aroni adaŵaŵerenga, monga momwe Chauta adaalamulira. Adaŵerenganso ana a Merari potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao, kuyambira anthu a zaka makumi atatu mpaka a zaka makumi asanu, onse amene ankatha kutumikira m'chihema chamsonkhano. Chiŵerengero chao chidakwanira 3,200 potsata mabanja ao. Ameneŵa ndiwo anthu a m'mabanja a Merari, anthu amene Mose ndi Aroni adaŵaŵerenga, monga momwe Chauta adaalamulira kudzera mwa Mose. Choncho Mose ndi Aroni, pamodzi ndi atsogoleri a Aisraele, adaŵaŵerenga Alevi onsewo potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Kuyambira anthu a zaka makumi atatu mpaka a zaka makumi asanu, onse amene ankatha kugwira ntchito yotumikira ndi yonyamula katundu wa m'chihema chamsonkhano, chiŵerengero chao chidakwanira 8,580. Anthuwo adaŵasankha kuti ena azigwira ntchito yotumikira, ndipo ena azinyamula katundu, monga momwe Chauta adaalamulira kudzera mwa Mose. Umu ndimo m'mene adaŵaŵerengera anthuwo, monga momwe Chauta adaamlamulira. Chauta adauza Mose kuti, “Lamula Aisraele kuti achotse wakhate aliyense m'zithando, aliyense wotulutsa zinthu zoipa m'thupi mwake, ndiponso munthu wodziipitsa pokhudza mtembo. Muchotse anthu onse otere, amuna kapena akazi. Muziŵatulutsira kunja kwa zithando kuti angaipitse zithando zao, poti Ine ndimakhala pakati pa anthu anga.” Tsono Aisraele adachitadi zimenezi, ndipo adaŵatulutsira kunja anthuwo. Ankachitadi monga momwe Chauta adaauzira Mose. Chauta adauza Mose kuti, “Uza Aisraele kuti, mwamuna kapena mkazi akachita munthu mnzake choipa chilichonse chimene anthu amati wochita zotere ndi wosakhulupirika kwa Chauta, munthuyo ndi wochimwadi. Aulule tchimo limene wachimwalo. Abweze zonse zimene adaononga, ndipo aonjeze chimodzi mwa zigawo zisanu za mtengo wake ndi kupatsa amene adamchimwirayo. Koma munthu akapanda kukhala ndi wachibale woti nkulandira zinthu zobwezedwa zija m'malo mwa zoonongedwazo, apereke zobwezedwazo kwa Chauta kuti zikhale za wansembe, kuwonjezera pa nkhosa yamphongo yadipo ija imene amachitira mwambo wopepesera machimo ake. Zopereka zonse zopatulika za Aisraele zimene amabwera nazo kwa wansembe, zikhale zake za wansembe. Zopereka zopatulika za munthu aliyense, nzake za iye yemweyo. Koma chilichonse chimene munthu apereka kwa wansembe, nchake cha wansembeyo.” Chauta adauza Mose kuti, “Uza Aisraele kuti, mwina mkazi adzazembera mwamuna wake namachita zosakhulupirika. Mwamuna wina atachita naye chigololo, zimenezo zitha kubisika, mwamuna wake osazidziŵa. Mkaziyo atha kukhala wosazindikirika kuti wadziipitsa, chifukwa chosoŵa mboni yomtsutsa, popeza kuti sadampezerere akuchita kumene. Pamenepo mwamuna wakeyo akayamba kuchitira nsanje mkazi wake amene wadziipitsayo, kapena akayamba kuchitira nsanje mkazi wakeyo ngakhale sadadziipitse, mwamunayo abwere ndi mkazi wakeyo kwa wansembe. Ndipo aperekere nsembe ya ufa wabarele wokwanira kilogaramu limodzi. Asathirepo mafuta kapena lubani pa nsembeyo, poti ndi chopereka cha chakudya choperekera nsanje, nsembe yotsutsa munthu, yoperekedwa kuti tchimo lakelo lizidziŵika. “Wansembe abwere ndi mkaziyo pafupi ndi kumuimika pamaso pa Chauta. Wansembeyo atengeko madzi oyera m'mbiya, ndipo atapeko fumbi la m'Chihema cha Mulungu ndi kulithira m'madzimo. Mkaziyo amuimike pamaso pa Chauta ndi kummasula tsitsi, ndipo aike m'manja mwake nsembe yaufa yachikumbutso, chopereka cha chakudya choperekera nsanje ija. Wansembeyo atenge madzi oŵaŵa m'manja mwake, madzi odzetsa matemberero. Tsono amlumbiritse mkaziyo kuti, ‘Ngati mwamuna wina aliyense sadagone nawe, ndipo ngati sudachite kanthu kokuipitsa pamene unali m'manja mwa mwamuna wako, madzi oŵaŵa ali apaŵa usatenge nawo matemberero. Koma ngati udamzemberapo mwamuna wako, ngakhale kuti unali m'manja mwake, nudziipitsa, ndipo ngati udagona ndi mwamuna wina wosakhala mwamuna wako,’ (apo wansembeyo amlumbiritse mkaziyo ndi mau amatemberero, ndi kumuuza kuti), ‘Chauta alisandutse dzina lako matemberero pakati pa anthu a mtundu wako Chauta afwapitse m'chiwuno mwako, ndi kutupitsa thupi lako. Madzi ali apa amatembereroŵa aloŵe m'matumbo mwako, atupitse thupi lako, ndipo afwapitse m'chiwuno mwako.’ Tsono mkaziyo avomere kuti, ‘Inde momwemo! Inde momwemo!’ “Wansembe alembe m'buku matemberero ameneŵa ndipo aŵafafanize poŵaviika m'madzi oŵaŵa aja. Mkaziyo ayenera kumwa madzi oŵaŵawo, madzi amatemberero, mpaka aloŵe m'mimba mwake, kuti amve ululu woopsa. Apo wansembe achotse m'manja mwa mkaziyo chopereka cha chakudya choperekera nsanje ija. Aipereke moweyula pamaso pa Chauta, ndipo abwere nayo ku guwa. Wansembe atapeko ufa wa dzanja limodzi kuti ukhale chikumbutso ndi kuutenthera pa guwa. Pambuyo pake apatse mkaziyo madzi aja kuti amwe. Mkazi atamwa madziwo, akakhala kuti adadziipitsa, kapena sadakhale wokhulupirika kwa mwamuna wake, madzi amatemberero aja adzaloŵa m'mimba mwake, ndipo iyeyo adzamva ululu woopsa. Thupi lake lidzatupa, m'chiwuno mwake mudzafwapa, ndipo mkaziyo adzakhala wotembereredwa pakati pa anthu a mtundu wake. Koma mkaziyo akakhala kuti sadadziipitse ndipo alibe tchimo, adzakhala wopanda mlandu, ndipo azidzabala ana. “Limeneli ndilo lamulo la za nsanje, pamene mkazi azembera mwamuna wake, nadziipitsa, ngakhale kuti ali m'manja mwa mwamuna wakeyo, kapena mwamuna akayamba kuchitira mkazi wake nsanje ndipo akumganizira zoipa. Mwamunayo amuimike mkazi wake pamaso pa Chauta, ndipo wansembe amchitire monga momwe lamulo likunenera. Mwamuna adzakhala wopanda tchimo lililonse, koma mkazi ndiye adzasenza tchimo lake.” Chauta adauza Mose kuti, “Uza Aisraele kuti pamene mwamuna kapena mkazi achita malumbiro apadera a unaziri, kuti adzipereke kwa Chauta, asamwe vinyo kapena chakumwa choledzeretsa. Asamwe vinyo wopangidwa ndi mphesa kapena chakumwa choledzeretsa, ndipo asamwe madzi amphesa kapena kudya mphesa zaziŵisi kapena zouma. Masiku onse pamene munthuyo ali wodzipereka kwa Chauta, asadye chilichonse chochokera ku mphesa, ngakhale mbeu zake kapena makungu ake. “Pa masiku onse amene adalumbira kuti adzakhala wodzipereka kwa Chauta, asamete kumutu kwake ndi lumo. Adzakhale wake wa Chauta nthaŵi zonse mpaka atatha masiku ake odzipereka kwa Chauta. Alilekerere tsitsi lake kuti likule. “Masiku onse pamene munthuyo wadzipereka kwa Chauta, asayandikire mtembo. Asadziipitse poyandikira mtembo wa bambo wake, wa mai wake, wa mbale wake kapena wa mlongo wake, chifukwa kulumbira kwa kudzipereka kwake kwa Mulungu kuli pamutu pake. Munthuyo ndi wopatulikira Chauta masiku onse a kudzipereka kwake. “Ngati munthu wina aliyense afa mwadzidzidzi pafupi naye, ndipo pakutero aipitsa tsitsi lake loperekedwalo, amete kumutu kwake pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, tsiku lomuyeretsa. Pa tsiku lachisanu ndi chitatu abwere ndi nkhunda ziŵiri kapena njiŵa ziŵiri kwa wansembe pakhomo pa chihema chamsonkhano. Wansembeyo apereke imodzi kuti ikhale nsembe yopepesera machimo, inayo ikhale ya nsembe yopsereza. Tsono amchitire mwambo wopepesera machimo ake, chifukwa adalakwa poyandikana ndi mtembo. Tsiku lomwelo aperekenso tsitsi lake kwa Chauta, mwiniwakeyo akhale wake wa Chauta masiku onse a kudzipereka kwake. Tsono abwere ndi mwanawankhosa wamphongo wa chaka chimodzi, kuti aperekere nsembe yopepesera kupalamula. Koma masiku a kudzipereka kwake koyamba kuja asaŵerengere, chifukwa kudzipereka kwakeko adakuipitsa. “Lamulo la Mnaziri pamene nthaŵi ya kudzipereka kwake yatha, nali: abwere naye pakhomo pa chihema chamsonkhano, ndipo iye apereke mphatso zake kwa Chauta. Apereke mwanawankhosa wamphongo wa chaka chimodzi wopanda chilema, kuti akhale nsembe yopsereza. Apereke nkhosa imodzi yaikazi ya chaka chimodzi yopanda chilema, kuti ikhale nsembe yopepesera machimo, ndi nkhosa imodzi yamphongo yopanda chilema, kuti ikhale nsembe yachiyanjano. Aperekenso dengu la buledi wosafufumitsa, makeke a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, timitanda ta buledi wosafufumitsa topyapyala ndi topaka mafuta, pamodzi ndi zopereka zake za zakudya ndi zachakumwa. Tsono wansembe abwere nazo zonsezo pamaso pa Chauta. Poyamba apereke nsembe yake yopepesera machimo ndi nsembe yake yopsereza. Atatero, apereke nkhosa yamphongo kwa Chauta, kuti ikhale nsembe yachiyanjano, pamodzi ndi dengu la buledi uja wosafufumitsa. Kenaka aperekenso chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa. Mnaziriyo amete kumutu kwake koperekedwa kuja pakhomo pa chihema chamsonkhano. Ndipo atenge tsitsi la ku mutu wake woperekedwawo, ndi kulitentha pa moto umene uli pansi pa nsembe yachiyanjano. Tsono wansembe atenge mwendo wamwamba wa nkhosa yamphongo wophika, ndipo atengenso keke imodzi yosatupitsidwa, pamodzi ndi mtanda umodzi wa buledi wosatupitsidwa, ndipo aziike m'manja mwa Mnaziri, atameta tsitsi lake loperekedwa lija. Ndipo wansembeyo azipereke moweyula, kuti zikhale nsembe zoweyula pamaso pa Chauta. Zimenezi nzoyera, zokhalira wansembe, pamodzi ndi nganga yoperekedwa moweyula ija. Pambuyo pake Mnaziri angathe kumwa vinyo. “Limeneli ndilo lamulo la munthu amene alumbira kuti akhale Mnaziri. Zinthu zake zimene apereka kwa Chauta zikhale zomwe adalumbirira pa unaziri, osaŵerengera zina zimene angathe kupereka moonjezerapo. Zimene adalumbira kuti adzachita, achite momwemo potsata lamulo la kudzipereka kuti adzakhale Mnaziri.” Chauta adauza Mose kuti, “Uza Aroni ndi ana ake kuti azidalitsa Aisraele motere: Chauta akudalitseni, ndipo akusungeni. Chauta akuyang'aneni mwachikondi ndipo akukomereni mtima. Chauta akuyang'aneni mwachifundo, ndipo akupatseni mtendere.” Ndipo Chauta adati, “Akamadzatchula dzina langa podalitsa Aisraele, Ine ndidzaŵadalitsadi.” Pa tsiku limene Mose adamaliza kumangitsa chihema cha Mulungu, nachidzoza ndi kuchipatula, pamodzi ndi zipangizo zake, adadzozanso guwa lansembe ndi kulipatula pamodzi ndi ziŵiya zake zomwe. Tsiku lomwelo akulu a Aisraele, ndiye kuti atsogoleri a mabanja ndi a mafuko amene ankayang'anira kuŵerenga kuja, adatenga zopereka zao, ndipo adabwera nazo pamaso pa Chauta. Adapereka ngolo zophimbidwa zisanu ndi imodzi ndiponso ng'ombe khumi ndi ziŵiri: atsogoleri aŵiri ngolo imodzi, ndipo mtsogoleri aliyense ng'ombe imodzi. Zimenezo adafika nazo ku chihema cha Chauta. Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Ulandire zimenezi kwa anthuwo kuti zithandize potumikira m'chihema chamsonkhano. Uŵapatse Alevi zimenezo, aliyense zoyenera ntchito yake.” Choncho Mose adatenga ngolo ndi ng'ombe zija nazipereka kwa Alevi. Ana a Geresoni adaŵapatsa ngolo ziŵiri ndi ng'ombe zinai potsata ntchito yao. Ana a Merari adaŵapatsa ngolo zinai ndi ng'ombe zisanu ndi zitatu potsata ntchito yao, imene woyang'anira wake anali Itamara, mwana wa wansembe Aroni. Koma ana a Kohati sadaŵapatse kanthu, chifukwa iwowo anali ndi ntchito yosamala zinthu zoyera zimene ankanyamulira pa phewa. Pambuyo pake atsogoleri adabwera ndi zopereka zopatulira guwa pa tsiku lomwe adalidzozalo. Ndipo adafika nazo zopereka zao patsogolo pa guwalo. Apo Chauta adauza Mose kuti, “Atsogoleriwo azibwera ndi zopereka zao zopatulira guwa, mtsogoleri mmodzi pa tsiku.” Nasoni mwana wa Aminadabu, wa fuko la Yuda, ndiye adapereka zopereka zake pa tsiku loyamba. Adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wolemera magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, zoperekera za zakudya. Adaperekanso kambale kamodzi kagolide kolemera magaramu 110, kodzaza ndi lubani. Adaperekanso mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa mmodzi wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza. Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo. Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali izi: ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zimene zinali zopereka za Nasoni mwana wa Aminadabu. Netanele mwana wa Zuwara, mtsogoleri wa fuko la Isakara, adapereka zopereka zake pa tsiku lachiŵiri. Zopereka zake zinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, zoperekera za zakudya. Adaperekanso kambale kamodzi kagolide ka magaramu 110, kodzadza ndi lubani, mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa imodzi yamphongo, ndiponso mwanawankhosa mmodzi wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza. Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo. Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zisanu zamphongo, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zinali zopereka za Netanele mwana wa Zuwara. Tsiku lachitatu linali la Eliyabu mwana wa Heloni mtsogoleri wa Azebuloni. Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, zoperekera za zakudya. Adaperekanso kambale kamodzi kagolide kolemera magaramu 110, kodzaza ndi lubani, mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa mmodzi wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza. Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo. Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zinali zopereka za Eliyabu mwana wa Heloni. Tsiku lachinai linali la Elizuri mwana wa Sedeuri, mtsogoleri wa Arubeni. Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wolemera magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta ndi zopereka za zakudya. Adaperekanso kambale kamodzi kagolide kolemera magaramu 110, kodzaza ndi lubani, mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa imodzi yamphongo, ndiponso mwanawankhosa mmodzi wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza. Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo. Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa amphongo asanu a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zinali zopereka za Elizuri mwana wa Sedeuri. Tsiku lachisanu linali la Selumiele mwana wa Zurishadai, mtsogoleri wa Asimeoni. Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, za chopereka cha chakudya. Adaperekanso kambale kamodzi kagolide ka magaramu 110, kodzaza ndi lubani, mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa mmodzi wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza. Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo. Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zinali zopereka za Selumiele mwana a Zurishadai. Tsiku lachisanu ndi chimodzi linali la Eliyasafu mwana wa Deuwele mtsogoleri wa Agadi. Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, za chopereka cha chakudya. Adaperekanso kambale kamodzi kagolide ka magaramu 110, kodzaza ndi lubani, mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa mmodzi wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza. Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo. Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zinali zopereka za Eliyasafu mwana wa Deuwele. Tsiku lachisanu ndi chiŵiri linali la Elisama mwana wa Amihudi, mtsogoleri wa Aefuremu. Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, za chopereka cha chakudya. Adaperekanso kambale kamodzi kagolide ka magaramu 110, kodzaza ndi lubani, mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa mmodzi wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza. Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo. Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zimene zinali zopereka za Alisama mwana wa Amihudi. Tsiku lachisanu ndi chitatu linali la Gamaliele mwana wa Pedazuri, mtsogoleri wa Amanase. Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, za chopereka cha chakudya. Adaperekanso kambale kamodzi kagolide ka magaramu 110, kodzaza ndi lubani, mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa mmodzi wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza. Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo. Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zimene zinali zopereka za Gamaliele mwana wa Pedazuri. Tsiku lachisanu ndi chinai linali la Abidani mwana wa Gideoni, mtsogoleri wa Abenjamini. Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, za chopereka cha chakudya. Adaperekanso kambale kamodzi kagolide ka magaramu 110, kodzaza ndi lubani, mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa mmodzi wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza. Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo. Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zimene zinali zopereka za Abidani mwana wa Gideoni. Tsiku lakhumi linali la Ahiyezere mwana wa Amishadai, mtsogoleri wa Adani. Iye adapereka mbale yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, za chopereka cha chakudya. Adaperekanso kambale kamodzi kagolide ka magaramu 110, kodzaza ndi lubani, mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza. Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo. Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zinali zopereka za Ahiyezere mwana wa Amishadai. Tsiku la 11 linali la Pagiyele mwana wa Okarani, mtsogoleri wa fuko la Asere. Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, za chopereka cha chakudya. Adaperekanso kambale kamodzi kagolide ka magaramu 110, kodzaza ndi lubani, mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza. Adaperekanso tonde mmodzi woperekera nsembe yopepesera machimo. Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zimene zinali zopereka za Pagiyele mwana wa Okarani. Tsiku la 12 linali la Ahira mwana wa Enani, mtsogoleri wa Anafutali, Iye adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wa magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, za chopereka cha chakudya. Adaperekanso kambale kamodzi kagolide ka magaramu 110, kodzadza ndi lubani, mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa yamphongo imodzi, ndiponso mwanawankhosa wamphongo wa chaka chimodzi, kuti zonsezo aperekere nsembe yopsereza; tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo. Ndipo zoperekera nsembe yachiyanjano zinali ng'ombe ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ndi anaankhosa asanu amphongo a chaka chimodzi. Zimenezi ndizo zinali zopereka za Ahira mwana wa Enani. Zopereka zopatulira guwa zimene atsogoleri a Aisraele adapereka pa tsiku limene guwalo lidadzozedwa, nazi: adapereka mbale zasiliva khumi ndi ziŵiri, mikhate yasiliva khumi ndi iŵiri, timbale tagolide khumi ndi tiŵiri. Mbale yasiliva iliyonse inkalemera kilogaramu limodzi ndi theka, ndipo mkhate uliwonse unkalemera magaramu 800. Siliva yense wa zipangizo zimenezo, ankalemera makilogaramu 27 ndi theka, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Timbale khumi ndi tiŵiri tagolide todzaza ndi lubani timene tinkalemera kalikonse magaramu 110, potsata muyeso wa ku malo opatulika, tonse pamodzi tinkalemera ngati kilogaramu limodzi ndi theka. Nyama zonse zoperekera nsembe zopsereza zinali ng'ombe zamphongo khumi ndi ziŵiri, nkhosa zamphongo khumi ndi ziŵiri, anaankhosa amphongo a chaka chimodzi khumi ndi aŵiri, pamodzi ndi chopereka cha chakudya, ndiponso atonde khumi ndi aŵiri operekera nsembe zopepesera machimo. Ndipo nyama zonse za nsembe zachiyanjano zinali ng'ombe zamphongo 24, nkhosa zamphongo 60, atonde 60, ndi anaankhosa amphongo a chaka chimodzi 60. Zimenezi ndizo zinali zopereka zopatulira guwa atalidzoza. Tsono Mose ataloŵa m'chihema chamsonkhano kukalankhula ndi Chauta, adamva mau kuchokera pa chivundikiro chokhala pamwamba pa Bokosi laumboni, pakati pa akerubi. Mulungu adalankhula naye. Chauta adauza Mose kuti, “Uza Aroni kuti, pamene ukuika nyale, uike zisanu ndi ziŵiri, ndipo ziwunikire patsogolo pa choikaponyale.” Aroni adaikadi nyalezo. Adaziika kuti ziwunikire patsogolo pa choikaponyale, monga momwe Chauta adaalamulira Mose. Choikaponyalecho adachipanga motere: chinali chagolide, ndipo kuyambira patsinde pake mpaka ku maluŵa ake, chinali chosula. Adapanga choikaponyalecho potsata chitsanzo chomwe Chauta adaaonetsa Mose. Chauta adauza Mose kuti, “Upatule Alevi pakati pa Aisraele, ndipo uŵayeretse. Kuŵayeretsa kwake uchite motere: uŵawaze madzi oyeretsera machimo ao. Amete m'thupi monse ndi lumo, ndipo achape zovala kuti adziyeretse. Tsono iwowo atenge mwanawang'ombe wamphongo, pamodzi ndi chopereka cha chakudya wosalala wosakaniza ndi mafuta. Iweyo utenge mwanawang'ombe wina wamphongo woperekera nsembe yopepesera machimo. Ubwere ndi Alevi pakhomo pa chihema chamsonkhano, ndipo usonkhanitse mpingo wonse wa Aisraele. Pamene ukuŵapereka Aleviwo pamaso pa Chauta, Aisraele asanjike manja ao pa Alevi. Kenaka Aroni apereke Aleviwo pamaso pa Chauta, kuti akhale chopereka choweyula cha Aisraele, kuti ntchito ya Alevi ikhaledi yotumikira Chauta. Pambuyo pake Alevi asanjike manja ao pamitu ya ng'ombe zamphongo, ndipo iwe upereke kwa Chauta ng'ombe imodzi kuti ikhale nsembe yopepesera machimo. Inayo uipereke kuti ikhale nsembe yopsereza, kuchitira mwambo wopepesera machimo a Alevi. Uŵauze Aleviwo kuti azitumikira Aroni ndi ana ake aamuna, ndipo uŵapereke kwa Chauta ngati chopereka choweyula. “Umu ndi m'mene upatulire Alevi pakati pa Aisraele, ndipo adzakhala anga. Pambuyo pake Aleviwo adzaloŵa kuti atumikire m'chihema chamsonkhano, utaŵayeretsa ndi kuŵapereka ngati chopereka choweyula. Ndithudi, iwoŵa aperekedwa kwathunthu kwa Ine pakati pa Aisraele. Ndaŵatenga kuti akhale anga m'malo mwa ana onse oyamba kubadwa, ana achisamba onse a Aisraele. Ana onse oyamba kubadwa pakati pa Aisraele ndi anga, ana a anthu ndi a nyama omwe. Ndidaŵapatula onseŵa kuti akhale anga, pa tsiku limene ndidapha ana onse oyamba kubadwa m'dziko la Ejipito. Tsono pakati pa Aisraele ndaŵatenga Alevi m'malo mwa ana onse oyamba kubadwa. Aleviwo ndaŵatenga pakati pa Aisraele ndi kuŵapereka ngati mphatso kwa Aroni ndi ana ake aamuna, kuti azidzatumikira m'malo mwa Aisraele, m'chihema chamsonkhano. Azikachita mwambo wopepesera machimo a Aisraele, kuti mliri ungaŵagwere Aisraele amene ayandikire pafupi ndi malo opatulika.” Umu ndimo m'mene Mose ndi Aroni ndi mpingo wonse wa Aisraele, adaŵachitira Alevi. Aisraele adachitira Aleviwo zonse monga momwe Chauta adaalamulira Mose. Alevi adadziyeretsa ku zoipa, ndipo adachapa zovala zao. Aroni adaŵapereka kuti akhale chopereka choweyula pamaso pa Chauta, naŵachitira mwambo wopepesera machimo ao, kuti aŵayeretse. Pambuyo pake Alevi adapita kukagwira ntchito zao m'chihema chamsonkhano, ndipo ankatumikira Aroni ndi ana ake. Choncho Aleviwo adaŵachitira monga momwe Chauta adaalamulira Mose. Chauta adauza Mose kuti, “Ntchito za Alevi ndi izi: kuyambira anthu a zaka 25 ndi opitirirapo, azipita kukagwira ntchito yotumikira m'chihema chamsonkhano. Akafika zaka makumi asanu aleke ntchito yotumikira, ndipo asatumikirenso. Koma azithandiza abale ao m'chihema chamsonkhano ndi kumayang'anira ntchitoyo, koma asatumikire. Umu ndimo m'mene udzachitire poŵagaŵira ntchito zao Aleviwo.” Pa mwezi woyamba wa chaka chachiŵiri Aisraele atatuluka m'dziko la Ejipito, Chauta adauza Mose m'chipululu cha Sinai kuti, “Aisraele azichita Paska pa nthaŵi yake. Muzichita Paska tsiku la 14 la mwezi uno, madzulo ake. Muzichita Paskayo potsata malamulo ake ndi malangizo ake onse.” Choncho Mose adauza Aisraele kuti azichita Paska. Ndipo Aisraele adachita Paska pa mwezi woyamba pa tsiku la 14, madzulo ake, m'chipululu cha Sinai. Adachita Paska monga momwe Chauta adaalamulira Mose. Panali anthu ena amene anali atadziipitsa chifukwa chokhudza mtembo wa munthu, kotero kuti sadathe kuchita nao Paska pa tsikulo. Motero adabwerera kwa Mose ndi kwa Aroni pa tsiku lomwelo. Anthuwo adauza Mose kuti, “Ife ndife oipitsidwa chifukwa tidakhudza mtembo wa munthu. Chifukwa chiyani tikuletsedwa kubwera ndi zopereka zathu kwa Chauta pa nthaŵi yake pakati pa anzathu Aisraele?” Mose adayankha kuti, “Dikirani kuti ndimve zimene Chauta alamule za inu.” Chauta adauza Mose kuti, “Uza Aisraele kuti, munthu wina aliyense mwa inu, kapena mwa zidzukulu zanu, akadziipitsa pokhudza mtembo wa munthu, kapena akakhala paulendo, achitebe Paska ya Chauta. Achite pa mwezi wachiŵiri, pa tsiku la 14, madzulo ake. Adye nyama ya Paskayo pamodzi ndi buledi wosafufumitsa ndi ndiwo zoŵaŵa zamasamba. Asasiyeko nyamayo mpaka m'maŵa kapena kuphwanya mafupa ake. Achite Paskayo potsata malamulo ake onse. Koma munthu amene sadadziipitse ndipo sali paulendo, komabe akana kuchita Paska, ameneyo achotsedwe pakati pa Aisraele, chifukwa sadabwere ndi zopereka zake kwa Chauta pa nthaŵi yake. Ameneyo adzalangidwa chifukwa cha tchimo lake. Mlendo akakhala pakati panu, nafuna kuchita nao Paska ya Chauta, nayenso achite Paskayo potsata malamulo ake ndi malangizo ake. Kaya ndinu alendo kapena ndinu mbadwa, nonse mukhale ndi lamulo limodzi lokha.” Pa tsiku limene adamanga malo opatulika, mtambo udaphimba malo opatulikawo, ndiye kuti chihema chaumboni chija. Madzulo aliwonse mpaka m'maŵa mwake, mtambowo unkaphimba malo opatulika uli ndi maonekedwe a moto. Zinkachitika motero mosalekeza. Mtambowo unkaphimba chihema chamsonkhano masana, ndipo usiku unkaoneka ngati moto. Mtambowo ukangokwera kuchoka pachihemapo, Aisraele ankanyamuka ulendo; ndipo pamene mtambowo unkakaima, Aisraele ankamanga mahema ao pamalo pamenepo. Aisraele ankanyamuka ulendo wao Chauta akaŵalamula, ndipo ankamanga mahema ao Chauta akaŵalamula. Nthaŵi yonse pamene mtambowo unali pa chihemacho, iwo ankakhalabe m'mahema. Ngakhale mtambowo ukhale masiku ambiri pamwamba pa chihemacho, Aisraele ankasungabe lamulo la Chauta, ndipo sankanyamuka. Nthaŵi zina mtambowo unkaphimba masiku oŵerengeka, ndipo Aisraele ankakhalabe m'mahema potsata malamulo a Chauta. Tsono ankanyamuka ulendo Chauta akaŵalamula. Nthaŵi zina mtambowo unkangophimba chihemacho kuyambira madzulo mpaka m'maŵa. M'maŵa mwake mtambowo ukachoka, iwo ankanyamuka ulendo wao. Mwina mtambowo unkaphimba chihema chija tsiku lonse ndi usiku womwe, koma ukangochokapo, iwowo ankanyamuka ulendo wao. Ngakhale mtambowo uphimbe pamwamba pa chihema cha Mulungu nkumakhala pomwepo masiku aŵiri kapena mwezi, kapena chaka, kapena nthaŵi yopitirirapo, Aisraele ankakhalabe m'mahema, ndipo sankanyamuka. Koma mtambowo ukangochokapo, iwo ankanyamuka ulendo. Aisraele ankamanga mahema ao Chauta akaŵalamula, ndipo ankanyamuka ulendo wao Chauta akaŵalamula. Ankasunga lamulo la Chauta, loŵafikira kudzera mwa Mose. Chauta adauza Mose kuti, “Upange malipenga aŵiri asiliva, uchite kusula. Uziimba malipengawo poitana mpingo, ndi pochoka pa mahema. Akaliza aŵiri onsewo, mpingo wonse usonkhane kwa iwe pa chipata cha chihema chamsonkhano. Koma akangoliza limodzi lokha, atsogoleri a mafuko a Aisraele ndiwo asonkhane kwa iwe. Mukaliza lipenga lochenjeza, anthu a m'mahema akuvuma ayambepo ulendo. Mukaliza lipenga lochenjeza kachiŵiri, anthu a m'mahema akumwera ayambepo ulendo. Muziŵalizira lipenga lochenjezalo nthaŵi zonse akamanyamuka ulendo. Pamene mpingo wonse uyenera kusonkhana pamodzi, mulize lipenga, koma musalize lipenga lochenjeza. Ana a Aroni, ansembe aja, ndiwo aziliza malipenga. Ntchito ya malipengayi ndi lamulo lamuyaya pa mibadwo yanu yonse. Pamene mukukamenya nkhondo m'dziko mwanu ndi adani amene akukuzunzani, nthaŵi imeneyo mulize malipenga ochenjeza, kuti Chauta wanu akukumbukeni, ndipo adzakupulumutsani kwa adani anu. Pa tsiku lanu losangalala, pa masiku osankhidwa a zikondwerero zanu, ndi pa masiku oyamba a miyezi, mulize malipenga pamene mukupereka nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zanu zachiyanjano. Malipengawo adzakuthandizani kumkumbukira Mulungu wanu. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.” Pa chaka chachiŵiri, mwezi wachiŵiri, tsiku la 20, mtambo udachoka pa chihema chaumboni. Tsono Aisraele adanyamuka ulendo wao m'magulumagulu kuchokera ku chipululu cha Sinai. Mtambowo udakaima m'chipululu cha Parani. Kameneka kanali koyamba kuti Aisraele anyamuke, Chauta atalamula kudzera mwa Mose. Otsata mbendera ya zithando za fuko la Yuda ndiwo adayamba kunyamuka m'magulumagulu, ndipo mtsogoleri wa gulu lao anali Nasoni mwana wa Aminadabu. Mtsogoleri wa gulu la fuko la Isakara anali Netanele mwana wa Zuwara. Mtsogoleri wa gulu la fuko la Zebuloni anali Eliyabu mwana wa Heloni. Anthu atagwetsa chihema cha Mulungu, ana a Geresoni ndi ana a Merari, oyenera kunyamula chihema cha Mulungu, adanyamuka ulendo wao. Pambuyo pake otsata mbendera ya zithando za fuko la Rubeni adanyamuka m'magulumagulu, ndipo mtsogoleri wa gulu lao anali Elizuri mwana wa Sedeuri. Mtsogoleri wa gulu la Asimeoni anali Selumiele mwana wa Zurishadai. Mtsogoleri wa gulu la fuko la Agadi anali Eliyasafu mwana wa Deuwele. Tsono Akohati atasenza zinthu zopatulika, adanyamuka. Malo opatulika anali atamangidwiratu iwowo asanafike. Otsata mbendera ya zithando za fuko la Efuremu adanyamuka m'magulumagulu, ndipo mtsogoleri wa gulu lao anali Elisama mwana wa Amihudi. Mtsogoleri wa gulu la fuko la Manase anali Gamaliele mwana wa Pedazuri. Mtsogoleri wa fuko la Abenjamini anali Abidani mwana wa Gideoni. Potsiriza otsata mbendera ya zithando za Adani amene anali kumbuyo kwa anthu a mahema onse, adanyamuka m'magulumagulu, ndipo mtsogoleri wa gulu lao anali Ahiyezere mwana wa Amishadai. Mtsogoleri wa gulu la fuko la Asere anali Pagiyele mwana wa Okarani. Mtsogoleri wa gulu la fuko la Nafutali anali Ahira mwana wa Enani. Umenewu ndiwo mndandanda wa kayendedwe ka Aisraele, pamene ankanyamuka ulendo wao m'magulumagulu. Mose adauza Hobaba, mwana wa Reuele Mmidiyani, mpongozi wake uja, kuti, “Tikupita ku malo amene Chauta adati, ‘Ndidzakupatsani.’ Tiyeni tipite limodzi, ndipo tidzakuchitirani zabwino, pakuti Chauta walonjeza Aisraele zinthu zabwino.” Koma iye adayankha kuti, “Sindipita nao, ndipita kwathu kwa abale anga.” Ndipo Mose adati, “Musatisiye, ndapota nanu, poti inu mukudziŵa kumene tingamange mahema m'chipululu muno, ndipo mudzakhala maso athu. Mukapita nao, zilizonse zimene Chauta adzatichitire, ife tidzakuchitirani zomwezo.” Choncho adanyamuka ku phiri la Chauta, nayenda ulendo wa masiku atatu. Bokosi lachipangano la Chauta lidatsogola, nayenda nalo ulendo wa masiku atatu, kuti akapeze malo oti anthu onse aja akapumuleko. Mtambo wa Chauta unkaŵaphimba masana, nthaŵi iliyonse pamene ankanyamuka pamahemapo. Nthaŵi iliyonse pamene Bokosi lachipangano linkanyamuka, Mose ankati, “Dzambatukani, Inu Chauta, muŵamwaze adani anu. Onse odana nanu athaŵe akakuwonani.” Mtambowo ukaima, Mose ankati, “Inu Chauta, bwererani kwa Aisraele anu amene ali zikwi zosaŵerengeka.” Tsiku lina anthu adadandaula, Chauta alikumva. Chauta atamva zimenezo, adapsa mtima, ndipo moto wa Chautayo udayaka pa anthuwo, nupsereza mbali imodzi ya mahema ao. Tsono anthu adalira kwa Mose, ndipo Moseyo atapemphera kwa Chauta, pompo motowo udazilala. Motero malowo adaŵatcha Tabera, chifukwa choti moto wa Chauta udayaka pakati pao. Nthaŵi imeneyo anthu ena osokoneza amene anali pakati pa Aisraele adamva nkhuli yaikulu. Aisraelenso adayamba kudandaula, adati, “Ndani adzatipatsa nyama kuti tizidya? Tikukumbukira nsomba zaulere zimene tinkadya ku Ejipito, minkhaka ija, mavwende ndi anyezi wamitundu-mitundu. Koma tsopano mphamvu zathu zatha, ndipo sitikuwona kanthu kena kakudya koma mana basi.” Manayo ankafanafana ndi njere za mapira, ndipo maonekedwe ake anali ngati ulimbo wouma. Anthu ankapita kukatola manayo, namapera pa mphero kapena kusinja mu mtondo, ndipo ankaphika, namapangira makeke. Kukoma kwake kunali ngati makeke ophika ndi mafuta. Pamene mame ankagwa usiku pamahemapo, ankagwera kumodzi ndi mana. Mose adaŵamva anthu aja akulira m'mabanja mwao monse, aliyense atakhala pakhomo pa hema lake. Chauta adaapsa mtima kwambiri, ndipo nayenso Mose adaaipidwa nazo. Mose adafunsa Chauta kuti, “Chifukwa chiyani mwandivutitsa chotere mtumiki wanune? Chifukwa chiyani simudandikomere mtima, mpaka kundisenzetsa katundu wa anthu onseŵa? Kodi ndidaatenga pathupi pa anthu onseŵa ndine? Kodi ndidaŵabala ndine, kuti Inu muzindiwuza kuti ndiŵafungate pachifuwa panga, monga momwe mlezi amachitira poyamwitsa mwana, ndipo kuti ndipite nawo ku dziko limene mudalonjeza makolo ao molumbira kuti mudzaŵapatsa? Kodi nyama yoti ndiŵapatse anthu onseŵa, ndiitenga kuti? Iwowo akundilirira ine kuti, ‘Tipatseni nyama, tidye.’ Ine sindingathe kuŵasamala ndekha anthu onseŵa. Katundu ameneyu sindingathe kumsenza. Ndipotu mukafuna kundichita zimenezi, mungondipha basi, ngati mwandikomera mtima, kuti ndisaonenso mavutowo.” Chauta adauza Mose kuti, “Usonkhanitse amuna makumi asanu ndi aŵiri mwa akuluakulu a Aisraele, anthu amene ukuŵadziŵa kuti ndi atsogoleri ndi akapitao a anthu. Ubwere nawo ku chihema chamsonkhano, ndipo aime kumeneko pamodzi ndi iwe. Ine nditsika kudzalankhula nawe komweko. Ndidzatengako mzimu uli pa iwe ndi kuuika pa iwowo. Ndipo adzasenza nawe katundu wa anthuwo, kuti usasenzenso wekha. Uŵauze anthuwo kuti, ‘Mudziyeretse, kukonzekera zamaŵa, ndipo mudzadya nyama. Inuyo mudalira Chauta alikumva, pamene munkati, “Ndani atipatse nyama tidye? Paja zinthu zinkatiyendera bwino ku Ejipito.” Nchifukwa chake Chauta adzakupatsani nyama, ndipo mudzadya. Simudzaidya tsiku limodzi lokha, kapena masiku aŵiri okha, kapena masiku asanu okha, kapena masiku khumi okha, kapena masiku makumi aŵiri okha ai. Imeneyo mudzaidya mwezi wathunthu, mpaka izikachita kutulukira m'makutu, inuyo nkumadwala nayo. Zimenezi zidzachitika chifukwa choti mwakana Chauta amene amakhala pakati panu, ndipo mwadandaula pamaso pake nkumati, “Chifukwa chiyani tidatuluka ku Ejipito?” ’ ” Koma Mose adati, “Anthu amene ndikuyenda nawoŵa akukwanira 600,000. Ndipo Inu mwanena kuti, ‘Ndiŵapatsa nyama kuti adye mwezi wathunthu.’ Kodi zidzaphedwa nkhosa kapena ng'ombe zingati kuti ziŵakwanire? Ngakhale nsomba zonse zam'nyanja, kodi zingathe kukwanira?” Chauta adafunsanso Mose kuti, “Kodi dzanja la Chauta ndi lalifupi? Tsono uwona lero lomwe lino, ngati zichitikadi monga momwe ndanenera kapena ai.” Choncho Mose adatuluka nakauza anthu mau a Chauta aja. Adasonkhanitsa anthu makumi asanu ndi aŵiri mwa akuluakulu a Aisraele, naŵakhazika mozungulira chihema chamsonkhano. Tsono Chauta adatsika mu mtambo nayamba kulankhula ndi Mose. Ndipo adatengako mzimu umene unali pa Moseyo nauika pa akuluakulu makumi asanu ndi aŵiriwo. Anthuwo atalandira mzimu uja, adayamba kulosa. Koma sadapitirire kulosako. Anthu aŵiri adatsalira m'mahema, wina anali Elidadi, wina Meladi, ndipo mzimu udakhala pa iwowo. Anali nao m'gulu la olembedwa aja, koma sadapite nao ku chihema chamsonkhano, motero ankalosera m'mahema. Ndiye mnyamata wina adathamanga nakauza Mose kuti, “Elidadi ndi Meladi akulosa kumahemaku.” Apo Yoswa, mwana wa Nuni, mtumiki wa Mose, mmodzi mwa anthu ake osankhidwa aja, adati, “Mbuyanga Mose, aletseni amenewo.” Koma Mose adamuuza kuti, “Kodi ukuchita nsanje chifukwa cha ine? Ndikadakondwa anthu onse a Chauta akadakhala aneneri, ndipo Chauta akadaika mzimu wake pa iwo.” Tsono Mose ndi atsogoleri a Aisraele aja adabwerera ku mahema. Tsono Chauta adautsa mphepo kuchokera ku nyanja. Mphepoyo idabwera ndi zinziri, ndipo zidagwera pafupi ndi mahema. Kuchokera kumahemako, zinzirizo zidagwa pa mtunda woyenda ulendo wa tsiku limodzi mbali imodzi, mbali inanso chimodzimodzi, mozungulira mahemawo. Zitaunjikana, mjintchi wake unali ngati mita limodzi kuchokera pansi mpaka pamwamba. Anthu atadzuka, ankagwira zinzirizo masana onse ndi usiku. M'maŵa mwakenso tsiku lathunthu, adachita chimodzimodzi. Panalibe ndi mmodzi yemwe amene adagwira zinziri zochepera makilogaramu chikwi chimodzi. Ndipo adaziyanika kuzungulira mahema onsewo. Nyama ikadali m'kamwa mwao, asanaimeze nkomwe, Chauta adaŵapsera mtima anthuwo, ndipo adaŵagwetsera mliri woopsa. Nchifukwa chake malowo adaŵatcha Mandaankhuli, chifukwa choti kumeneko ndiko kumene adakwirira anthu ankhuli. Kuchokera ku Mandaankhuliko, anthu adapita ku Hazeroti, ndipo adakhala komweko. Miriyamu ndi Aroni adayamba kumnena Mose chifukwa cha mkazi wachikusi amene Moseyo adamkwatira, poti adakwatiradi mkazi wa ku Kusi. Iwowo adafunsa kuti, “Kodi nzoona kuti Chauta adalankhula kudzera mwa Mose yekha? Kodi sadalankhulenso kudzera mwa ife?” Chauta adazimva zimenezo. Koma Mose anali munthu wofatsa kupambana anthu onse a pa dziko lapansi. Tsono Chauta adauza Mose, Aroni ndi Miriyamu kuti, “Atatu nonsenu mubwere ku chihema chamsonkhano.” Ndipo onse atatuwo adapitadi. Chauta adatsika mu mtambo, naima pakhomo pa hema, ndipo adaitana Aroni ndi Miriyamu, tsono aŵiri onsewo adabweradi. Chauta adati, “Imvani mau anga. Pakakhala mneneri pakati panupa, Ine Chauta ndimadziwonetsa kwa munthuyo m'masomphenya, ndimalankhula naye m'maloto. Koma sinditero ndi mtumiki wanga Mose, amene wakhala woyang'anira anthu anga onse a Israeli. Ndimalankhula naye pakamwampakamwa, momveka osati mophiphiritsa, ndipo amaona ulemerero wanga. Chifukwa chiyani tsono simudaope kumnena Mose, mtumiki wanga?” Pamenepo Chauta adaŵakwiyira, nachokapo. Mtambo utachoka pamwamba pa chihema, Miriyamu adapezeka ali ndi khate lambuu ngati ufa, ndipo Aroni atacheuka, adangoona Miriyamu ali ndi khate. Apo Aroni adauza Mose kuti, “Mbuyanga, musatilange chifukwa choti tachimwa, ndipo tachita zopusa. Musalole kuti Miriyamu akhale ngati mwana wobadwa wakufa, amene thupi lake lili loonongeka kumodzi.” Tsono mokweza mau Mose adauza Chauta kuti, “Mulungu ndikukupemphani kuti mumchiritse Miriyamu.” Koma Chauta adauza Mose kuti, “Bambo wake akadamthira malovu kumaso, kodi Miriyamu sakadachita manyazi masiku asanu ndi aŵiri? Basi, amtsekere kunja kwa mahema masiku asanu ndi aŵiri, ndipo pambuyo pake angathe kumloŵetsanso.” Choncho adamtsekera Miriyamu kunja kwa mahema masiku asanu ndi aŵiri. Ndipo anthu sadathe kunyamuka ulendo wao mpaka Miriyamu atamloŵetsanso. Pambuyo pake anthu aja adanyamuka ku Hazeroti nakamanga mahema ao ku chipululu cha Parani. Chauta adauza Mose kuti, “Tuma anthu kuti akazonde dziko la Kanani limene ndikupatsa Aisraele. Pa fuko lililonse utume munthu mmodzi, amene ali mtsogoleri m'fukolo.” Choncho Mose adaŵatuma kuchokera ku chipululu cha Parani, monga momwe Chauta adaalamulira, ndipo onsewo anali atsogoleri a Aisraele. Maina ao ndi aŵa: m'fuko la Rubeni, adatuma Samuwa mwana wa Zakuri. M'fuko la Simeoni, adatuma Safati mwana wa Hori. M'fuko la Yuda, adatuma Kalebe mwana wa Yefune. M'fuko la Isakara, adatuma Igala mwana wa Yosefe. M'fuko la Efuremu, adatuma Hoseya mwana wa Nuni. M'fuko la Benjamini, adatuma Paliti mwana wa Rafu. M'fuko la Zebuloni, adatuma Gadiele mwana wa Sodi. M'fuko la Yosefe (ndiye kuti m'fuko la Manase) adatuma Gadi mwana wa Susi. M'fuko la Dani, adatuma Amiyele mwana wa Gemali. M'fuko la Asere, adatuma Seturi mwana wa Mikaele. M'fuko la Nafutali, adatuma Nabi mwana wa Vofusi. M'fuko la Gadi, adatuma Geuwele mwana wa Maki. Ameneŵa ndiwo maina a anthu amene Mose adaŵatuma kukazonda dziko. Ndipo Hoseya mwana wa Nuni, Mose adamutcha dzina loti Yoswa. Mose adaŵatuma kukazonda dziko la Kanani, naŵauza kuti, “Pitani cha ku Negebu, ndipo mukakwere dziko lamapirilo. Mukaone dzikolo kuti ndi lotani, ndipo ngati anthu am'dzikomo ngamphamvu kapena opanda mphamvu, ngati ngoŵerengeka kapena ambiri. Mukaone ngati dziko limene akukhalamolo ndi labwino kapena loipa, ngati mizinda imene amakhalamo ndi yamahema kapena yamalinga. Mukaonenso ngati dzikolo ndi lolemera kapena losauka, ndipo ngati nkhalango zilimo kapena ai. Mulimbe mtima, ndipo mukabwere ndi zipatso zina zam'dzikomo.” Imeneyo inali nyengo yopsa mphesa zoyamba. Choncho adapita kukazonda dzikolo kuyambira ku chipululu cha Zini mpaka ku Rehobu pafupi ndi chipata cha Hamati. Adadzera njira ya ku Negebu nakafika ku Hebroni, kumene kunkakhala Ahimani, Sesai ndi Talimai, zidzukulu za Aanaki. (Adamanga Hebroni zaka zisanu ndi ziŵiri asanamange Zowani ku Ejipito.) Ndipo adafika ku chigwa cha Esikolo, nathyolako nthambi yokhala ndi tsango limodzi la mphesa, ndipo aŵiri mwa iwowo adainyamula mopika. Adatengakonso makangaza ndi nkhuyu. Malowo adaŵatcha chigwa cha Esikolo, chifukwa cha tsango lamphesa limene anthu aja adathyola kumeneko. Patapita masiku makumi anai, anthu aja adabwerako kumene adakazonda dziko kuja. Adabwera kwa Mose ndi Aroni ndi kwa mpingo wa Aisraele m'chipululu cha Parani ku Kadesi. Adasimbira Mose ndi Aroni ndi mpingo wonse za ulendo wao naŵaonetsa zipatso za ku dzikolo. Adaŵauza kuti, “Tidakafika kudziko kumene inu mudatituma. Dzikolo ndi lamwanaalirenji, zipatso zake ndi izi. Komatu anthu am'dzikomo ngamphamvu, mizinda yao ndi yozingidwa ndi malinga, ndiponso ndi yaikulu kwambiri. Kuwonjezera pamenepo, tidaonanso zidzukulu za Aanaki kumeneko. Aamaleke amakhala m'dziko lakumwera. Ahiti, Ayebusi ndi Aamori amakhala m'dziko lamapiri. Akanani amakhala m'mphepete mwa nyanja ndi m'mphepete mwa mtsinje wa Yordani.” Koma Kalebe adaŵakhalitsa chete anthu pamaso pa Mose, nati, “Tiyeni tipite nthaŵi yomwe ino, tikalande dzikolo, chifukwa tingathe kuligonjetsa.” Tsono anthu aja amene adaapita naye limodziŵa adati, “Sitingathe kukalimbana nawo anthuwo, poti ngamphamvu kopambana ife.” Choncho adasimbira Aisraelewo zoipa za dzikolo zimene adakaziwona, adati, “Dziko limene tidakalizondalo ndi dziko limene limaononga anthu ake. Ndipo anthu onse amene tidaŵaona kumeneko ngaataliatali. Tidaonanso ziphona, (zidzukulu za Aanaki). Ifeyo tinkaoneka ngati ziwala, ndipo iwonso ankatiwona ngati ziwala.” Pamenepo mpingo wonse udafuula kwambiri, ndipo anthu adalira usiku umenewo. Aisraele onse adayamba kuŵiringulira Mose ndi Aroni. Mpingo wonse udaŵauza kuti, “Kukadakhala bwino tikadangofera ku Ejipito, kapena m'chipululu mommuno. Chifukwa chiyani Chauta akutiloŵetsa m'dziko limenelo kuti tikaphedwe pa nkhondo? Akazi athu adzatengedwa ku ukapolo pamodzi ndi ana athu. Kodi sikukadakhala bwino koposa kuti tibwerere ku Ejipito?” Ndipo adayamba kuuzana kuti, “Tiyeni tisankhe mtsogoleri kuti tibwerere ku Ejipito.” Mose ndi Aroni adadziponya pansi pamaso pa mpingo wonse wa Aisraele. Yoswa mwana wa Nuni, ndi Kalebe mwana wa Yefune, amene adaali m'gulu la anthu okazonda dziko lija, adang'amba zovala zao. Ndipo adauza mpingo wonse wa Aisraele uja kuti, “Dziko limene tidakalizondalo ndi labwino kwambiri. Ngati Chauta amatikonda, adzatiloŵetsa m'dziko lamwanaalirenjilo ndi kutipatsa kuti likhale lathu. Koma musagalukire Chauta. Musaope anthu a m'dzikolo chifukwa tidzaŵaononga. Iwowo alibe oŵatchinjiriza, koma ife Chauta ali nafe, musaŵaope.” Koma mpingo wonse udaati uŵaponye miyala. Pomwepo ulemerero wa Chauta udaonekera Aisraele onse m'chihema chamsonkhano. Chauta adafunsa Mose kuti, “Kodi anthu ameneŵa adzaleka liti kundinyoza? Ndipo adzaleka liti kusandikhulupirira, ngakhale aone zizindikiro zimene ndachita pakati pao? Ndidzaŵapha ndi mliri ndi kuŵalanda choloŵa chao, ndipo iwe ndidzakusandutsa mtundu waukulu ndi wamphamvu kupambana iwoŵa.” Koma Mose adayankha Chauta kuti, “Zimenezitu Aejipito adzazimva, pakuti ndinu amene mudaŵatulutsa anthu ameneŵa m'dziko la Ejipito. Tsono Aejipito azidzasimbira anthu a m'dziko muno. Iwo amva kale kuti Inu Chauta muli pakati pa anthu ameneŵa. Inu Chauta mumaŵaonekera maso ndi maso, ndipo mtambo wanu umaŵaphimba. Masana mumaŵatsogolera ndi mtambo, usiku mumaŵatsogolera ndi moto. Tsopano mukaŵapha onse anthu ameneŵa, mitundu ina imene yamva mbiri yanu idzati, ‘Chauta waŵaphera m'chipululu anthuŵa, chifukwa choti sadathe kuŵaloŵetsa m'dziko limene adalumbira kuti adzaŵapatsa kuti likhale lao.’ Tsono ndikukupemphani, Chauta muwonetse kuti mphamvu zanu nzazikulu monga mudalonjezera kuti, ‘Chauta ndi wosakwiya msanga, ndi wodzaza ndi chifundo chosasinthika, ndi wokhululukira ochimwa ndi opalamula. Koma sadzaleka kulanga ochimwa, amalanga ana a mbadwo wachitatu ndi wachinai chifukwa cha kuchimwa kwa makolo ao.’ Ndikukupemphani kuti muŵakhululukire kuchimwa kwao anthu ameneŵa kaamba ka chifundo chanu chachikulu ndi chosasinthika, ndiponso chifukwa mwakhala mukuŵakhululukira anthu ameneŵa kuyambira ku Ejipito mpaka tsopano lino.” Chauta adati, “Ndaŵakhululukira chifukwa cha mau ako. Koma ndikulumbira kuti pali Ine ndemwe ndiponso malinga nkuti dziko lonse lapansi ndi lodzaza ndi ulemerero wa Chauta, Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaloŵe m'dzikolo. Anthu ameneŵa adaona ulemerero wanga ndi zizindikiro zanga zimene ndidachita ku Ejipito ndi m'chipululu muno, komabe adandipenekera kakhumi konse osamvera mau anga. Palibe amene adzaone dziko limene ndidalonjeza makolo ao molumbira kuti ndidzaŵapatsa. Mwa amene adandikana palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaliwone dzikolo. Koma Kalebe mtumiki wanga, chifukwa ali ndi mtima wosiyana ndi ena, ndipo wanditsata ndi mtima wonse, ndidzamloŵetsa m'dziko limene adapitamolo, ndipo zidzukulu zake zidzalandira dzikolo kuti likhale lao. Tsono popeza kuti Aamaleke ndi Akanani amakhala m'zigwa, maŵa mubwerere, muyambepo ulendo wopita ku chipululu, mudzere ku Nyanja Yofiira.” Chauta adafunsa Mose ndi Aroni kuti, “Kodi anthu oipa chotereŵa, adzaleka liti kundiŵiringulira? Ndamva maŵiringulo ao amene akundichitira. Uŵauze kuti, Chauta akunena kuti, ‘Zimene mwanena, Ine ndamva, ndipo ndi zimene ndidzakuchitani. Mitembo yanu idzakhala ili mbwee m'chipululu muno. Anthu onse, kuyambira a zaka makumi aŵiri ndi opitirirapo, amene adandiŵiringulira, palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaloŵe m'dziko limene ndidalumbira kuti mudzaloŵamo, kupatula Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni. Ana anu amene munkati adzagwidwa mu ukapolo, ndidzaŵaloŵetsa m'dzikomo, ndipo adzalidziŵa dziko limene inu mukunyozalo. Koma enanu, mitembo yanu idzakhala ili mbwee m'chipululu mommuno. Ana anu adzakhala abusa m'chipululu akungoyendayenda zaka makumi anai, ndipo adzasauka chifukwa cha kusakhulupirika kwanu, mpaka inuyo mutatha ndi kufa m'chipululu. Padzapita zaka makumi anai mukulangidwa chifukwa cha zolakwa zanu, kuŵerenga chaka chimodzi pa tsiku lililonse la masiku makumi anai aja amene munkazonda dziko. Mudzadziŵa kuwopsa kwake kwa kukangana ndi Ine.’ Ine Chauta ndanena. Ndithudi, ndidzachitadi zimenezi kwa anthu onse oipaŵa, amene agwirizana kuti andiwukire. M'chipululu mommuno ndimo m'mene athere, ndipo afera mommuno.” Anthu amene Mose adaŵatuma kuti akazonde dziko aja atabwerako, ena adayamba kuutsa mitima ya anthu kuti aukire Mose pakuŵauza zoipa za dzikolo. Anthu onsewo amene ankasimba zoipa za dzikolo, adafa ndi mliri pamaso pa Chauta. Koma mwa anthu amene adapita kukazonda dziko aja, Yoswa mwana wa Nuni ndi Kalebe mwana wa Yefune ndiwo adatsala amoyo. Mose adaŵafotokozera Aisraele mau onseŵa, ndipo anthu adalira kwambiri. Adalaŵirira m'mamaŵa, ndipo adakwera cha ku dziko lamapiri, nati “Ife pano takonzeka kukwera mpaka kukafika ku malo amene Chauta adatilonjeza. Ndithu tachimwadi.” Koma Mose adati, “Chifukwa chiyani mukunyoza lamulo la Chauta, poti zimenezo sizidzatheka? Musapite, kuti mungaphedwe pamaso pa adani anu, pakuti Chauta sali nanu. Kumeneko Aamaleke ndi Akanani ali m'tsogolo mwanu, ndipo mudzaphedwa pa khondo. Chauta sadzakhala nanu, chifukwa choti mwaleka kumtsata.” Koma iwo adapitabe osasamala, nakwera ku dziko lamapiri, ngakhale kuti sadatsakane ndi Bokosi lachipangano cha Chauta, kapena ndi Mose, pochoka pamahemapo. Tsono Aamaleke ndi Akanani, amene ankakhala m'dziko lamapirilo, adatsika ndipo adaŵagonjetsa, ndi kuŵapirikitsa mpaka ku Horoma. Chauta adauza Mose kuti, “Uza Aisraele kuti, ‘Mukadzaloŵa m'dziko limene ndidzakupatsenilo, mwina muzidzapereka ng'ombe kapena nkhosa kwa Chauta kuti zikhale nsembe yotentha pa moto, kapena yopsereza, kapena yopembedzera, kuti mukwaniritse zimene mudalonjeza molumbira. Mwina mudzazipereka kuti zikhale nsembe yaufulu kapena nsembe yopereka pa nthaŵi ya zikondwerero zosankhidwa, kuti zikhale nsembe zotulutsa fungo lokomera Chauta. Tsono amene adzabwere ndi zoperekayo, adzapereke kwa Chauta chopereka cha chakudya, cholemera kilogaramu limodzi, wosakaniza ndi mafuta okwanira lita limodzi. Adzaperekenso vinyo wa chopereka cha chakumwa wokwanira lita limodzi pa mwanawankhosa aliyense, kuwonjezera pa nsembe yopsereza kapena pa nsembe yopembedzera. Ikakhala nkhosa yamphongo, muzipereka chopereka cha chakudya cholemera makilogaramu aŵiri, wosakaniza ndi mafuta okwanira lita limodzi ndi theka. Pachopereka cha chakumwa, mudzapereka vinyo wokwanira lita limodzi ndi theka, kuti ikhale nsembe yotulutsa fungo lokomera Chauta. Pamene mupereka ng'ombe yamphongo kwa Chauta, kuti ikhale nsembe yopsereza kapena nsembe yopembedzera, kapena kuti zichitikedi zimene mudalumbira, kapena kuti ikhale nsembe yachiyanjano, muperekere kumodzi ndi ng'ombeyo chopereka cha chakudya cholemera makilogaramu atatu, wosakaniza ndi mafuta okwanira malita aŵiri. Pachopereka cha chakumwa mupereke vinyo wokwanira malita aŵiri, kuti ikhale nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta.’ “Umu ndimo m'mene zidzachitikire ndi ng'ombe yamphongo iliyonse, kapena nkhosa yamphongo, kapena mwanawankhosa aliyense kapena mwanawambuzi. Zingachuluke chotani nyama zoperekedwazo, muchite choncho ndi nyama iliyonse, mpaka zonse kutha. Mbadwa zonse zizichita motero pamene zikupereka nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta. Ngati ndi mlendo amene akhala pakati panu, kapena wina aliyense amene akhala pakati panu pa mibadwo yanu yonse, ndipo afuna kupereka nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta, azichita monga momwe muchitira inu. Kunena za msonkhano wonse, pakhale lamulo limodzi lokha kwa inu ndi kwa alendo amene akhale pakati panu, lamulo lamuyaya pa mibadwo yanu yonse. Monga momwe muliri inu, alendonso ali momwemo pamaso pa Chauta. Kwa inu ndi kwa mlendo wokhala pakati panu, pakhale lamulo limodzi ndi mwambo umodzi wokha.” Chauta adauza Mose kuti, “Uza Aisraele kuti, ‘Mukadzaloŵa m'dziko m'mene ndidzakufikitsani, ndipo mukamadzadya buledi wam'dzikolo, mudzapereke nsembe kwa Chauta. Pa buledi wanu woyamba, mudzaperekeko mmodzi kuti adzakhale nsembe. Mudzampereke monga momwe mumaperekera zopereka za popunthira tirigu. Muzidzapereka motero kwa Chauta buledi mmodzi mwa buledi wanu woyamba pa mibadwo yanu yonse.’ “Koma mwina mutha kulakwa mosadziŵa, osasunga malamulo onse amene Chauta adauza Mose, ndi zonse zimene adakulamulani kudzera mwa Mose, kuyambira tsiku limene Chauta adapereka lamulo mpaka m'tsogolo mwake pa mibadwo yanu yonse. Ngati cholakwacho chidachitika mosadziŵa, mpingo womwe osazindikira, pamenepo mpingo wonsewo upereke mwanawang'ombe wamphongo kuti akhale nsembe yopsereza, yotulutsa fungo lokomera Chauta. Apereke pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi chakumwa, potsata zimene ndidakulamulani. Aperekenso tonde kuti akhale nsembe yopepesera machimo. Wansembe achite mwambo wopepesera machimo a mpingo wonse wa Aisraele ndipo anthuwo adzakhululukidwa, chifukwa choti adalakwa mosadziŵa. Tsono atabwera ndi zopereka zao ngati nsembe yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta, ndiponso ngati nsembe yopepesera machimo, yopereka kwa Chauta, kuti azimpepesa pa cholakwa chao chija, mpingo wonse wa Aisraele udzakhululukidwa pamodzi ndi mlendo yemwe amene akhala pakati pao, poti anthu onse adalakwa mosadziŵa. “Ngati munthu mmodzi alakwa mosadziŵa, apereke mbuzi yaikazi ya chaka chimodzi kuti ikhale nsembe yopepesera machimo. Motero wansembe amchitire mwambo wopepesera machimo pamaso pa Chauta munthu wolakwa mosadziŵayo. Akalakwa choncho mosadziŵa, amchitire mwambo wopepesera machimo, ndipo adzakhululukidwa. Mukhale ndi lamulo limodzi pa munthu aliyense amene alakwa mosadziŵa, pa mbadwa iliyonse pakati pa Aisraele ndi pa mlendo amene akhala pakati pao. Koma munthu amene achimwa dala, ngakhale akhale mbadwa kapena mlendo, wanyoza Chauta, ndipo munthu ameneyo achotsedwe pakati pa anthu anzake. Popeza kuti wanyoza mau a Chauta ndipo waphwanya lamulo la Chauta, amchotseretu munthu ameneyo, tchimo lake lidzamkangamira.” Pamene Aisraele anali m'chipululu muja, adapeza munthu akutola nkhuni pa tsiku la Sabata. Amene adapeza munthuyo akutola nkhuni, adabwera naye kwa Mose ndi Aroni ndi kwa mpingo wonse. Iwo adamponya m'ndende chifukwa choti sankadziŵa bwino zoti amchite. Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Munthuyo aphedwe. Mpingo wonse umponye miyala kunja kwa mahema.” Pomwepo mpingo udamtulutsira kunja kwa mahema munthuyo ndi kumupha pomponya miyala, monga momwe Chauta adaalamulira Mose. Chauta adauza Mose kuti, “Lankhula ndi Aisraele, ndipo uŵauze kuti pa mibadwo yao yonse azisokerera mphonje pa ngodya za zovala, ndipo pa mphonje ya ngodya iliyonse asokerepo chingwe chobiriŵira. Mphonje imeneyo muzidzaiyang'ana ndi kumakumbukira malamulo onse a Chauta, kuti muziŵamvera, ndipo musamatsatenso zilakolako zokhota za mtima wanu kapena za maso anu zimene munkazitsata. Choncho mudzakumbukira ndi kugwiritsa ntchito malamulo anga onse, mudzakhala oyera mtima pamaso pa Mulungu wanu. Ine ndine Chauta amene ndidakutulutsani ku dziko la Ejipito, kuti ndikhale Mulungu wanu. Ine ndine Chauta.” Kora mwana wa Izara, mwana wa Kohati, mwana wa Levi, ndiponso Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu, pamodzi ndi Oni mwana wa Peleti, adzukulu a Rubeni, adakopa anthu. Adaukira Mose, iwowo pamodzi ndi atsogoleri a Aisraele 250, osankhidwa ndi anthu pa msonkhano, anthu otchuka. Onsewo adasonkhana pamodzi ndipo adaukira Mose ndi Aroni, naŵauza kuti, “Inu mwankitsa nazo. Mpingo wonse ndi woyera, munthu aliyense mumpingomo ndi wa Chauta, ndipo Chauta ali pakati pathu. Chifukwa chiyani tsono mukudziyesa opambana pa msonkhano wa Chauta?” Mose atamva zimenezi, adagwada napemphera, kenaka adauza Kora pamodzi ndi gulu lake lonse kuti, “Maŵa m'maŵa, Chauta atiwonetse amene ali wakewake, ndiponso amene ali woyera mtima, ndipo adzamuuza kuti abwere pafupi naye. Munthu amene Mulungu amsankheyo, adzamufikitsa pafupi. Tsono iwe Kora, pamodzi ndi gulu lako lonse, muchite izi: mutenge zofukizira lubani, muikemo moto, ndipo muthiremo lubani maŵa pamaso pa Chauta. Munthu amene Chauta amsankheyo, ndiye woyera wake. Inu Alevi, ndinu amene mwamkitsa nazo.” Mose adauza Kora kuti, “Imvani tsono inu Alevi. Kodi simukukhutira nazo zakuti Mulungu wa Israele adakupatulani mu mpingo wa Israele, kuti mubwere pafupi ndi Mulungu kudzatumikira m'Chihema chake, ndipo kuti muime pamaso pa msonkhano ndi kuŵatumikira anthuwo? Ndiponso kodi Mulungu adakulolani kuti mubwere pafupi ndi Iye, inu pamodzi ndi abale anu Alevi, amene ali nanu? Kodi mukukhumbiranso ndi unsembe womwe? Tsono kutereku nkukangana ndi Chauta, pamene iwe ndi gulu lako mwasonkhana chotere. Kodi Aroni ndiye yani kuti muzimuukira?” Apo Mose adatuma munthu kukaitana Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu. Ndipo iwo adati, “Ife sitibwera kumeneko. Kodi zikukucheperani kuti mudatitulutsa ku dziko lamwanaalirenji ku Ejipito, kuti tifere m'chipululu muno? Kodi mukufunanso kuti mukhale mfumu yathu yotilamula? Kuwonjezera apo, simudatiloŵetse m'dziko lamwanaalirenji, ndipo simudatipatse polima kapena minda yamphesa, kuti ikhale choloŵa chathu. Kodi mukufuna kutigwira m'maso? Ife sitibwera kumeneko.” Apo Mose adapsa mtima kwambiri, ndipo adauza Chauta kuti, “Musalandire nsembe za anthu ameneŵa. Sindidaŵalande ndi bulu mmodzi yemwe, ndipo sindidalakwire ndi mmodzi yemwe mwa iwo.” Tsono Mose adauza Kora kuti. “Maŵa iwe pamodzi ndi anthu a gulu lako 250, mubwere ku hema lamsonkhano, iweyo ndi anthu akowo ndi Aroni. Aliyense mwa inu atenge chofukizira lubani, athiremo lubani. Nonsenu mubwere ku chihemacho, aliyense ndi chofukizira chake. Zofukizirazo zikhale 250, ndipo iweyo ndi Aroni mutenge aliyense chakechake.” Choncho munthu aliyense adatenga chofukizira lubani, naikamo moto, ndi kuthiramo lubani, ndipo adakaimirira pa chipata cha chihema chamsonkhano, pamodzi ndi Mose ndi Aroni. Kora adasonkhanitsa mpingo wonse pa chipata cha chihema chamsonkhano moyang'anana ndi Mose ndi Aroni. Ndipo ulemerero wa Chauta udaonekera mpingo wonsewo. Ndipo Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti, “Chokani pakati pa mpingowu kuti ndiwononge onse nthaŵi imodzi.” Apo iwo adadziponya pansi, nati, “Inu Mulungu, Chauta mwini moyo wa anthu onse, kodi mukwiyira mpingo wonse chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodzi?” Chauta adauza Mose kuti, “Uza mpingo kuti achoke pafupi ndi mahema a Kora, Datani ndi Abiramu.” Tsono Mose adapita kwa Datani ndi Abiramu, ndipo akuluakulu a Aisraele adamtsatira. Mose adauza mpingowo kuti, “Ndapota nanu, chokani pakati pa mahema a anthu oipaŵa, ndipo musakhudze chinthu chao chilichonse, kuti angakuphereni kumodzi chifukwa cha zoipa zao.” Choncho anthuwo adachokapo pafupi ndi mahema a Kora, Datani ndi Abiramu. Pamenepo Datani ndi Abiramu adatuluka naima pakhomo pa mahema ao pamodzi ndi akazi ao, ana ao ndi makanda ao. Tsono Mose adati, “Pano muzindikira kuti ntchito zonse ndikuchitazi, adandituma ndi Chauta, si za m'mutu mwanga ai. Anthu aŵa akafa monga m'mene amafera anthu onse, Mulungu osaŵalanga, ndiye kuti Chauta sadanditume ai. Koma Chauta akachita chinthu china chachilendo, nthaka ikayasama ndi kuŵameza iwowo pamodzi ndi zinthu zao zonse, natsikira kumanda ali moyo, mpamene mudziŵe kuti anthu ameneŵa anyoza Chauta.” Mose atangomaliza kulankhula mau ameneŵa, nthaka idang'ambika pamene padaali iwopo. Nthakayo idayasama ndi kuŵameza onsewo pamodzi ndi mabanja ao ndiponso anthu onse a gulu la Kora ndi zinthu zao zonse. Motero iwowo adaloŵa m'manda ali moyo, pamodzi ndi zinthu zao zonse. Nthaka idaŵatsekera pansi, motero adazimirira pakati pa msonkhano wonse. Pomwepo Aisraele onse amene anali pafupi adathaŵa, atamva anthuwo akulira. Ankati, “Tiyeni tithaŵe kuti nthakayi ingatimeze nafenso.” Tsono padayaka moto wochokera kwa Chauta ndipo udapsereza anthu 250 amene ankafukiza lubani aja. Pambuyo pake Chauta adauza Mose kuti, “Uza Eleazara, mwana wa wansembe Aroni, kuti achotse zofukizira lubani zija m'motomo, ndipo motowo aumwazire kutali. Zofukizira za anthu amene aphedwa chifukwa cha kuchimwa kwao nzoyera. Zofukizirazo azisule chophimbira pa guwa, poti azipereka pamaso pa Chauta, nchifukwa chake nzoyera. Motero zidzakhala chizindikiro kwa Aisraele onse.” Choncho wansembe Eleazara adatenga zofukizira zamkuŵa zija zimene adadzapereka anthu amene adapsa ndi moto aja. Adazisula chophimbira pa guwa, kuti zikhale chikumbutso kwa Aisraele, kuti munthu aliyense amene sali wansembe, amene sali mmodzi mwa zidzukulu za Aroni, asayandikire kudzafukiza lubani pamaso pa Chauta, kuti zingamgwere zonga zimene zidagwera Kora ndi gulu lake. Zonse zidachitika monga momwe Chauta adauzira Eleazara kudzera mwa Mose. Koma m'maŵa mwake mpingo wonse wa Aisraele udaŵiringulira Mose ndi Aroni kuti, “Inu mwapha anthu a Chauta.” Pamene mpingo udasonkhana kuti uukire Mose ndi Aroni, anthuwo adatembenuka ndi kuyang'ana ku chihema chamsonkhano. Tsono adangoona mtambo utaphimba chihemacho, ndipo ulemerero wa Chauta udaonekera. Mose ndi Aroni adabwera patsogolo pa chihema chamsonkhano, ndipo Chauta adauza Moseyo kuti, “Choka pakati pa gulu la anthuli, kuti ndiŵaononge onse nthaŵi imodzi.” Aŵiriwo adadziponya pansi. Mose adauza Aroni kuti, “Tenga chofukizira lubani chako, ndipo uikemo moto wa pa guwa ndi kuthiramo lubani. Upite nacho msanga kumene kuli gulu la anthuko, ndipo uŵachitire mwambo wopepesera machimo ao. Inde, mkwiyo wa Chauta watsika, ndipo mliri wayamba kale.” Choncho Aroni adatenga chofukizira, nathamangira pakati penipeni pa msonkhano. Ndipo adangoona mliri utayamba kale pa anthuwo. Tsono adathira lubani, nachita mwambo wopepesera machimo a anthuwo. Aroni adakaima pakati pa anthu akufa ndi amoyo aja, ndipo mliriwo udaleka. Komabe amene adafa ndi mliriwo anali 14,700, kuwonjeza pa anthu aja amene adafa pa mlandu wa Kora. Pambuyo pake Aroni adabwerera kwa Mose ku chipata cha chihema chamsonkhano, mliriwo utaleka. Chauta adauza Mose kuti, “Ulankhule ndi Aisraele kuti akupatse ndodo, fuko lililonse ndodo imodzi. Atsogoleri ao onse akupatse ndodo khumi ndi ziŵiri molingana ndi mafuko a makolo ao. Ulembe dzina la munthu aliyense pa ndodo yake, ndipo ulembe dzina la Aroni pa ndodo ya Levi. Pakuti payenera kukhala ndodo imodzi pa mtsogoleri aliyense wa fuko la makolo ake. Tsono ndodozo uziike m'chihema chamsonkhano patsogolo pa bokosi laumboni pamene ndimakumana nawe. Ndipo ndodo ya munthu amene nditi ndimsankhe idzaphuka. Motero sindidzalola kumvanso maŵiringulo amene Aisraele amachita otsutsana nawe.” Choncho Mose adalankhula ndi Aisraele. Ndipo atsogoleri onse adampatsa ndodozo, mtsogoleri aliyense ndodo imodzi molingana ndi mafuko a makolo ao, ndiye kuti ndodo khumi ndi ziŵiri pamodzi. Ndodo ya Aroni inali pakati pa ndodo zao. Mose adakaziika ndodozo pamaso pa Chauta m'chihema chaumboni. M'maŵa mwake Mose adakaloŵa m'chihema chaumboni. Adangoona ndodo ya Aroni, ya fuko la Levi, itaphuka masamba nkuchitanso maluŵa, ndipo itabala zipatso zakupsa za mtundu wa matowo. Tsono Mose adatulutsa ndodo zonse zija pamaso pa Chauta ndi kuŵaonetsa Aisraele. Ataona, mtsogoleri aliyense adatenga ndodo yake. Apo Chauta adauza Mose kuti, “Kabwezere ndodo ya Aroni patsogolo pa bokosi laumboni. Uisunge kuti ikhale chenjezo kwa anthu oukira aja, kuti aleke kuŵiringulako, kuti angafe.” Mose adachita momwemo. Adatsatadi zomwe Chauta adalamula. Tsono Aisraele adauza Mose kuti, “Tatayika, tonsefe taferatu. Ngati munthu aliyense amene akuyandikira chihema cha Chauta alikufa, ndiye kuti tonsefe ndife akufa.” Pambuyo pake Chauta adauza Aroni kuti, “Iwe pamodzi ndi ana ako ndi banja la makolo ako pamodzi nawe, ndinu amene musenze zotsatira za tchimo lililonse lokhudza malo opatulika kwambiri. Ndipo iwe ndi ana ako, ndinu amene musenze zotsatira za tchimo lililonse lokhudza unsembe. Ubwere nawonso abale ako a fuko la Levi, fuko la kholo lako, kuti azigwira nawe ntchito, azikuthandiza iwe pamodzi ndi ana ako, pamene mukutumikira m'chihema chaumboni. Iwowo adzakutumikirani ndi kugwiranso ntchito zonse zam'chihema. Koma asadzafike pafupi ndi zipangizo za m'malo opatulika kapena guwa, kuti iwowo pamodzi ndi inuyo mungafe. Iwo adzagwira nawe ntchito, ndi kumatumikiranso m'chihema chamsonkhano pa ntchito zonse zam'chihemamo. Ndipo wina aliyense asadzafike pafupi ndi inu. Mudzatumikira pa ntchito za m'malo opatulika ndi pa ntchito za guwa, kuti mkwiyo usaŵagwerenso Aisraele. Ndaŵasankha abale ako, Alevi, pakati pa Aisraele. Iwowo ndi mphatso kwa iwe, aperekedwa kwa Chauta kuti azitumikira m'chihema chamsonkhano. Tsono iwe pamodzi ndi ana ako, muzitumikira pa ntchito zaunsembe, ntchito zonse zokhudza guwa, ndi pa ntchito zonse za m'malo opatulika kwambiri. Ndakupatsa unsembe ngati mphatso yako, koma munthu wina aliyense wofika pafupi, adzaphedwa.” Chauta adauzanso Aroni kuti, “Pa zopereka kwa Ine, ndakupatsa zotsala zimene amasunga, ndiye kuti zinthu zimene Aisraele amapatulira Ine. Ndakupatsa zimenezi kuti zikhale gawo lako ndi la ana ako, kuti zikhale zanu mpaka muyaya. Mwa zopereka zoyera kopambana zimene sadazitenthe pa guwa, zanu zikhale izi: chepereka chonse cha chakudya, nsembe zao zonse zopepesera machimo ndi nsembe zao zonse zopepesera kupalamula, zimene amapereka kwa Ine, zonsezo zikhale zoyera kwa iwe ndi kwa ana ako. Muzidyera ku malo opatulika kopambana. Mwamuna aliyense angathe kudyako. Zimenezi nzoyera kwa inu. Zinanso zanu ndi izi: zopereka zao zamphatso, ndi zopereka zoweyula za Aisraele. Zimenezi ndazipereka kwa iwe, kwa ana ako aamuna, ndi kwa ana ako aakazi amene ali ndi iwe, kuti zikhale zanu mpaka muyaya. Munthu aliyense amene ali wosaipitsidwa angathe kudyako. Ndakupatsani mafuta onse abwino kopambana, vinyo yense ndi mbeu zonse zabwino kwabasi, ndi zipatso zonse zoyamba zimene anthu amapereka kwa Chauta. Mwa zinthu zonse za m'dziko mwako, zipatso zoyambirira kupsa zimene amapereka kwa Chauta, zimenezo zikhale zanu. Munthu aliyense wosaipitsidwa m'nyumba mwanu angathe kudyako. Chinthu chilichonse chimene anthu amapatulira Chauta m'dziko la Israele chikhale chanu. Chinthu chilichonse choyamba kubadwa, kaya ndi munthu kaya nyama, chimene amapereka kwa Chauta, chikhale chanu, Komabe mwana wamwamuna wachisamba muzimuwombola, ndiponso pakati pa nyama zosayenera kuzipereka ku nsembe, mwana wake woyamba kubadwa muzimuwombola. (Muzimuwombola akakhala wa mwezi umodzi). Uike mtengo wake woombolera kuti ukhale ndalama zisanu zasiliva, molingana ndi ndalama za ku malo opatulika. Koma mwanawang'ombe woyamba kubadwa kapena mwanawankhosa woyamba kubadwa, kapenanso mwanawambuzi woyamba kubadwa, musaŵaombole. Amenewo ngoyera. Muwaze magazi ao pa guwa, ndipo mutenthe mafuta ao kuti akhale nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta. Koma nyama yake ikhale yako, monga momwe imakhalira nganga yoweyula, ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja. Zopereka zonse zoyera zimene Aisraele amapereka kwa Chauta ndakupatsa iwe, ana ako aamuna ndi ana ako aakazi ali ndi iwe. Zimenezi zikhale zako mpaka muyaya. Chimenechi ndicho chipangano chamuyaya pamaso pa Chauta, chochita ndi iwe ndi ana ako.” Ndipo Chauta adauza Aroni kuti, “Iwe udzakhala wopanda choloŵa m'dziko mwao, ndiponso udzakhala wopanda gawo lililonse pakati pao. Ine ndine gawo lako ndi choloŵa chako pakati pa Aisraele. “Ndaŵapatsa Alevi chachikhumi chilichonse m'dziko la Israele kuti chikhale chigawo chao, chifukwa cha ntchito imene akuigwira m'chihema chamsonkhano. Kuyambira tsopano Aisraele asamafika pafupi ndi chihema chamsonkhano, kuti angachimwe ndipo angafe. Koma Alevi ndiwo amene azitumikira m'chihema chamsonkhano, ndipo adzalangidwa ngati alakwa pa udindo wao. Limeneli likhale lamulo pa mibadwo yanu yonse. Aleviwo asakhale ndi chigawo pakati pa Aisraele. Tsono chachikhumi chimene Aisraele amapereka kwa Chauta, ndapatsa Aleviwo kuti chikhale chigawo chao. Nchifukwa chake ndaŵauza kuti asadzakhale ndi chigawo pakati pa Aisraele.” Chauta adauza Mose kuti, “Uŵauzenso Alevi kuti, ‘Pamene mulandira kwa Aisraele chachikhumi chimene ndakupatsani kuti chikhale chigawo chanu, muperekeko chachikhumi cha chachikhumicho kuti chikhale nsembe kwa Chauta. Ndipo chopereka chanucho chidzaŵerengedwa ngati tirigu woyamba kucha amene anthu amapuntha, ndiponso mphesa zoyamba kucha zimene amapsinya. Choncho inunso muzipereka zopereka zanu kwa Chauta, zotapa pa chachikhumi chilichonse chimene mulandira kwa Aisraele. Pa zimene mwalandirazo mutengeko mphatso ya Chauta, ndipo mupatse wansembe Aroni. Pa mphatso zonse zimene mwalandira, mupatuleko zake za Chauta, ndipo zimene mwapatulazo zikhale zabwino kopambana zina zonse.’ Nchifukwa chake uŵauze kuti, ‘Mutaperekako zabwino kopambana zina zonse, zotsalazo muziŵerengere kuti nzanu, monga tirigu woyamba kucha amene anthu amapuntha, ndiponso mphesa zoyamba kucha zimene amapsinya. Mungathe kuzidyera pa malo aliwonse, inuyo ndi a m'banja mwanu. Zimenezo ndi mphotho yanu chifukwa cha ntchito imene mumagwira m'chihema chamsonkhano. Ndipo simudzachimwa mukadya zimenezo, ngati mwapereka kale kwa Chauta zabwino kopambana zina zonse. Motero simudzanyoza zinthu zoyera za Aisraele ndipo simudzafa.’ ” Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti, “Lamulo limene Chauta wapereka nali: Muuze Aisraele kuti abwere ndi msoti wa ng'ombe wofiira, wosapunduka, wopanda chilema, ndiponso umene sudasenzepo goli chiyambire. Muupereke kwa wansembe Eleazara, kenaka anthu atuluke nawo kunja kwa mahema, ndipo auphe pamaso pake. Tsono wansembe Eleazara atengeko magazi a ng'ombeyo ndi chala chake, ndipo awaze magaziwo kumaso kwa chihema chamsonkhano kasanunkaŵiri. Ng'ombeyo aitenthe, Eleazara akupenya. Chikopa chake, nyama yake, magazi ake pamodzi ndi ndoŵe yake, azitenthe zonsezo. Wansembe atenge mtengo wa mkungudza, kachitsamba ka hisope ndi kansalu kamlangali, ndipo zonsezo aziponye m'moto m'mene ng'ombe ija ikunyekamo. Tsono wansembe achape zovala zake, ndipo asambe thupi lonse, pambuyo pake aloŵe m'mahema. Koma wansembeyo adzakhale woipitsidwa mpaka madzulo. Munthu amene atentha ng'ombeyo achape zovala zake, ndipo asambe thupi lonse, koma adzakhalebe woipitsidwa mpaka madzulo. Munthu amene ali wosaipa pa zachipembedzo ndiye aole phulusa la ng'ombelo, ndipo aliike kunja kwa mahema pa malo aukhondo pa zachipembedzo. Asungire mpingo wa Aisraele phulusalo, kuti aziika m'madzi oyeretsera zonyansa pa zachipembedzo. Mwambo umenewu ndi wochotsera tchimo. Munthu amene aola phulusa la ng'ombe achape zovala, koma iyenso adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo. Limeneli likhale lamulo lamuyaya kwa Aisraele ndi kwa mlendo wokhala pakati pao. “Amene akhudza mtembo wa munthu wina aliyense, akhala woipitsidwa masiku asanu ndi aŵiri. Asambe ndi madzi oyeretsera aja pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri kuti ayere, ndipo adzamuyeretsadi. Koma akapanda kusamba pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku lachisanu ndi chiwiri kuti ayere, sadzayera. Munthu aliyense wokhudza munthu wakufa, ndipo sadziyeretsa, munthu ameneyo akuipitsa Chihema cha Chauta, choncho adzachotsedwa m'dziko la Aisraele. Akhale woipitsidwa chifukwa sadawazidwe madzi aja oyeretsera pa zachipembedzo, ndi woipitsidwabe ameneyo. “Pamene munthu afera m'hema, lamulo lake nali: munthu aliyense amene aloŵa m'hemamo, ndipo aliyense amene ali m'hema, akhale woipitsidwa masiku asanu ndi aŵiri. Ndipo chiŵiya chilichonse chopanda chivundikiro nchoipitsidwa. Munthu aliyense amene akhudza munthu wophedwa ndi lupanga panja, kapena mtembo, kapena fupa la munthu wakufa, kapenanso manda, akhala woipitsidwa masiku asanu ndi aŵiri. Woipitsidwayo amtengereko m'mbiya phulusa la nsembe yopsereza yopepesera machimo, ndipo aonjezemo madzi abwino atsikulo. Tsono munthu wosaipitsidwa atenge kachitsamba ka hisope ndi kukaviika m'madzi aja, ndipo awaze madziwo pa hema, pa zipangizo zake zonse, pa anthu amene anali m'menemo, ndi pa munthu amene adakhudza fupa la munthu wakufa, kapena munthu wophedwa, kapena chikulu mtembo kapena manda. Munthu wosaipitsidwayo awaze madzi munthu woipitsidwa uja, pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri. Atawazidwa madzi choncho pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, achape zovala zake, asambe thupi lonse, ndipo madzulo ake adzakhala woyeretsedwa. “Koma munthu woipitsidwa akapanda kudziyeretsa, ameneyo achotsedwe pakati pa msonkhano, pakuti waipitsa malo opatulika a Chauta. Ameneyo ndi woipitsidwa chifukwa sadamuwaze madzi oyeretsera aja. Limeneli likhale lamulo lamuyaya kwa iwo. Munthu amene awaza madzi oyeretserawo, achape zovala zake. Ndipo munthu amene akhudza madzi ochapirawo, adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo. Chinthu chilichonse chimene munthu woipitsidwa akhudza, chidzakhala choipitsidwa. Ndipo munthu aliyense wokhudza chimenecho, adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo.” Pa mwezi woyamba, mpingo wonse wa Aisraele udafika ku chipululu cha Zini, ndipo anthuwo adakhala ku Kadesi. Miriyamu adafera kumeneko naikidwa komweko. Kumeneko kunalibe madzi oti mpingowo umwe. Tsono anthu adasonkhana pamodzi naukira Mose ndi Aroni. Anthuwo adayamba kukangana ndi Mose, adati, “Kukadakhala bwino tikadafera pamodzi ndi abale athu aja amene adafa pamaso pa Chauta. Chifukwa chiyani mwafikitsa mpingo wa Chauta kuchipululu kuno, kuti ife tifere kuno pamodzi ndi zoŵeta zathu? Ndipo chifukwa chiyani mudatitulutsa m'dziko la Ejipito ndi kutifikitsa ku malo oipa ano? Kuno sikumera tirigu kapena mitengo ya mikuyu, kapena mitengo ya mipesa, kapenanso mitengo ya makangaza, ndipo kulibe ndi madzi akumwa omwe.” Apo Mose ndi Aroni adachoka pa msonkhano uja, napita ku khomo la chihema chamsonkhano, ndipo adadziponya pansi. Pomwepo ulemerero wa Chauta udaŵaonekera. Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Tenga ndodo, ndipo iwe ndi mbale wako Aroni musonkhanitse mpingo, tsono ulamule thanthwe kuti litulutse madzi, anthu akuwona. Motero udzaŵatulutsira madzi m'thanthwe anthuwo, ndipo udzamwetsa mpingo wonsewo ndi zoŵeta zao zomwe.” Pamenepo Mose adatenga ndodo imene inali pamaso pa Chauta, monga momwe Iyeyo adamlamulira. Tsono Mose ndi Aroni adasonkhanitsa mpingo wonse pamodzi kuthanthweko nauza anthuwo kuti, “Imvani anthu opandukanu. Kodi tichite kukutulutsirani madzi m'thanthwemu?” Apo Mose adakweza dzanja lake, namenya thanthwe kaŵiri ndi ndodo yake. Pompo mudatuluka madzi ambiri, ndipo mpingo wonsewo udamwa pamodzi ndi zoŵeta zomwe. Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti, “Popeza kuti simudandikhulupirire, ndipo simudasonyeze pamaso pa Aisraele kuti ndine woyera, simudzaŵaloŵetsa anthuŵa m'dziko limene ndaŵapatsa.” Ameneŵa ndiwo madzi a ku Meriba kumene Aisraele adakangana ndi Chauta, ndipo Chauta adadziwonetsa pakati pa anthuwo kuti ndi woyera. Ali ku Kadesi, Mose adatuma amithenga kwa mfumu ya ku Edomu kuti akanene kuti, “Abale anu Aisraele akuti, ‘Mukudziŵa mavuto onse amene atigwera, Pajatu makolo athu adaapita ku Ejipito, ndipo tidakhala kumeneko zaka zambiri. Aejipito adatizunza ife ndi makolo athu. Titalira kwa Chauta, adamva kulira kwathu, natuma mngelo amene adatitulutsa m'dziko la Ejipitolo. Tsopano tili kuno ku Kadesi, mzinda umene uli m'malire a dziko lanu. Mutilole tsono tidzere m'dziko mwanu. Sitidzera m'minda mwanu kapena m'mipesa mwanu. Ndipo sitidzamwa madzi a m'zitsime zanu. Tidzangodzera mu mseu wanu waukuluwo basi, mpaka titadutsa dziko lanu.’ ” Koma Edomu adayankha kuti, “Musadzere kuno, kuti ndingafike kudzakubayani ndi lupanga.” Aisraele adamuuza kuti, “Ife tidzangodzera mu mseu waukulu mokhamo. Ngati ife ndi zoŵeta zathu timwako madzi anu, tidzalipira. Mungotilola kuti tidutse chabe.” Koma Edomu adaŵayankha kuti, “Simudutsa ai.” Pamenepo Edomu adatuluka ndi gulu lankhondo lalikulu ndi lamphamvu kukalimbana ndi Aisraele. Motero Edomu sadavomere kuti Aisraele adutse m'dziko mwake. Ndipo Aisraele adadzera njira ina. Tsono mpingo wonse wa Aisraele udanyamuka ku Kadesi kuja nukafika ku phiri la Horo. Ku phiri limenelo, limene lili m'malire a dziko la Edomu, Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti, “Aroni saloŵa nao m'dziko limene ndidapatsa Aisraele. Adzafa, chifukwa choti nonse aŵirinu simudamvere lamulo langa ku madzi a ku Meriba kuja. Utenge Aroni pamodzi ndi Eleazara mwana wake, ukwere nawo pamwamba pa phiri la Horo. Kumeneko umvule Aroni zovala zaunsembe ndi kuveka mwana wake Eleazara. Ndipo Aroni adzafera komweko.” Mose adachitadi zimene Chauta adamlamula. Atatu onsewo adakwera phiri la Horo, mpingo wonse ukupenya. Apo Mose adamuvula Aroni zovala zake zaunsembe, naveka Eleazara mwana wake. Ndipo Aroni adafera pamwamba pa phiri pomwepo. Tsono Mose ndi Eleazara adatsika phiri. Pamene mpingo udamva kuti Aroni wamwalira, mpingo wonse wa Israele udalira maliro a Aroni masiku makumi atatu. Mfumu Yachikanani ya ku Aradi imene inkakhala kumwera, itamva kuti Aisraele akubwera, kudzera njira ya ku Atarimu, idathira nkhondo Aisraelewo, nigwirako ena ukapolo. Tsono Aisraele adalumbira kwa Chauta kuti, “Ngati muŵapereka anthu ameneŵa m'manja mwathu, ife tidzaonongeratu mizinda yao.” Chauta adamvera mau a Aisraelewo naŵaperekadi Akanani aja m'manja mwao. Aisraele adaŵaonongeratu Akananiwo pamodzi ndi mizinda yao yomwe. Choncho malowo adaŵatcha kuti Horoma. Aisraele adanyamuka ku phiri la Horo nadzera njira ya ku Nyanja Yofiira, kuzungulira dziko la Edomu. Koma pa njira adayamba kunyong'onyeka. Anthu aja adayamba kuŵiringulira Mulungu ndiponso Mose, adati, “Chifukwa chiyani mudatitulutsa m'dziko la Ejipito kuti tidzafere m'chipululu muno? Pakuti kuno kulibe ndi chakudya chomwe ngakhalenso madzi, ndipo chakudya chachabechi chatikola.” Tsono Chauta adatumiza njoka za ululu wonga moto pakati pa anthu aja, ndipo zidaŵaluma, kotero kuti Aisraele ambiri adafa. Ndipo anthu adabwera kwa Mose, namuuza kuti, “Pepani tidachimwa poti tidakangana ndi Chauta ndi inu nomwe. Mupemphere kwa Chauta kuti atichotsere njokazi.” Choncho Mose adaŵapempherera anthuwo. Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Upange njoka yamkuŵa, ndipo uipachike pa mtengo. Aliyense wolumidwa akangoiyang'ana njokayo, adzakhala moyo.” Choncho Mose adapanga njoka yamkuŵa, naipachika pa mtengo. Ndiye ankati wina aliyense njoka ikamuluma, munthuyo akayang'ana njoka yamkuŵa ija, ankakhala moyo. Aisraele adanyamukanso, nakamanga mahema ao ku Oboti. Ndipo adachoka ku Oboti nakamanga ku Iyeabarimu m'chipululu choyang'anana ndi Mowabu, kuvuma. Atachoka kumeneko, adakamanga m'chigwa cha Zeredi. Kuchokera kumeneko adakamanga patsidya pa mtsinje wa Arinoni umene uli m'chipululu chochokera ku malire a dziko la Amori. Mtsinje wa Arinoni umene ndiwo malire a Mowabu, uli pakati pa dziko la Mowabu ndi dziko la Amori. Nchifukwa chake buku la nkhondo za Chauta limanena kuti, “Mzinda wa Waheba uli ku Sufa, ku zigwa za Arinoni, ku matsitso a zigwa amene afika mpaka ku Ari, nakhudza malire a dziko la Mowabu.” Kuchokera kumeneko adapitirira mpaka ku malo oti Beeri. Chimenecho chinali chitsime chimene Chauta adaalozera Mose namuuza kuti, “Uŵasonkhanitse pamodzi anthuwo, ndipo ndidzaŵapatsa madzi.” Tsono Aisraele adaimba nyimbo iyi yakuti, “Tulutsa madzi ako, chitsime iwe, ife tiŵaimbira nyimbo! Chitsime chimene adakumba mafumu, chimene atsogoleri omveka a anthu adakumba, adakumba ndi ndodo zao zaufumu ndiponso ndi ndodo zao zoyendera.” Kuchokera kuchipululu, Aisraele adafika ku Matana, kuchokera ku Matana adafika ku Nahaliyele, kuchokera ku Nahaliyele adafika ku Bamoti. Kuchokera ku Bamoti adafika ku chigwa cha m'dziko la Mowabu, kudzera njira ya pamwamba pa phiri la Pisiga, loyang'anana ndi chipululu cham'munsi. Tsono Aisraele adatuma amithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, kukanena kuti, “Mutilole kuti tidzere m'dziko mwanumo. Sitidzadzera m'minda mwanu, kapena m'mipesa mwanu. Sitidzamwa madzi a m'chitsime chanu. Tidzangotsata mseu wanu waukulu mpaka titadutsa dziko lanulo.” Koma Sihoni sadalole kuti Aisraele adutse dziko lake. Adasonkhanitsa anthu ake onse pamodzi, napita kukamenyana nkhondo ndi Aisraele kuchipululu, ndipo adafika ku Yahazi, namenyana ndi Aisraele. Ndipo Aisraele adamgonjetsa ndi lupanga, nalanda dziko lake kuyambira ku mtsinje wa Arinoni mpaka ku mtsinje wa Yaboki, kufikira m'malire a dziko la Aamori, chifukwa malirewo anali otchinjirizidwa. Aisraele adalanda mizinda yonseyi nakhala m'mizinda yonse ya Aamori, ku Hesiboni ndi m'midzi yake yonse. Hesiboni unali mzinda wa Sihoni mfumu ya Aamori, amene adaamenyana ndi mfumu yakale ya Amowabu, ndipo adamlanda dziko lake lonse mpaka ku mtsinje wa Arinoni. Nchifukwa chake oimba ndakatulo amati, “Bwerani ku Hesiboni, mzindawu umangidwenso, tiyeni timange mzinda wa Sihoni kuti ukhazikikenso. Moto udabuka ku Hesiboni. Malaŵi a moto adatuluka mu mzinda wa Sihoni. Moto udaononga Ari mzinda wa ku Mowabu, udapserezeratu mapiri a kumtunda kwa Arinoni. Tsoka kwa iwe Mowabu, mwatha inu anthu opembedza Kemosi. Ana ake aamuna waasandutsa othaŵathaŵa, ana ake aakazi waasandutsa akapolo, akapolo a Sihoni mfumu ya Aamori. Choncho zidzukulu zao zidatha nkufa, kuyambira ku Hesiboni mpaka ku Diboni, ndipo tidaŵaononga mpaka ku Nofa, pafupi ndi Medeba.” Motero Aisraele adakhala m'dziko la Aamori. Mose adatuma anthu kuti akazonde Yazere. Ndipo Aisraele adagwira midzi yake, napirikitsa Aamori amene anali kumeneko. Tsono adabwerera, nadzera njira ya ku Basani. Ogi mfumu ya ku Basaniko adatuluka kukalimbana nawo. Iyeyo pamodzi ndi anthu ake onse adakamenyana nawo nkhondo ku Ederei. Koma Chauta adauza Mose kuti, “Usamuwope. Ndampereka m'manja mwako pamodzi ndi anthu ake onse ndi dziko lake lomwe. Ndipo umchite zomwe udachita Sihoni mfumu ya Aamori amene ankakhala ku Hesiboni.” Choncho Aisraele adapha Ogi, ana ake aamuna ndi anthu ake onse, kotero kuti panalibe ndi mmodzi yemwe amene adatsalira, ndipo adalanda dziko lakelo. Aisraele adanyamuka ulendo nakamanga mahema ao m'zigwa za Amowabu patsidya pa Yordani ku Yeriko. Balaki mwana wa Zipora adaona zonse zimene Aisraele adachita Aamori. Amowabu adaopa anthuwo kwambiri, chifukwa anali ambirimbiri. Amowabu adachitadi mantha ndi Aisraele. Choncho Amowabuwo adauza akuluakulu a ku Midiyani kuti, “Tsopano khamu limeneli libudula zonse zimene zatizungulira, monga momwe ng'ombe zimabudulira udzu wam'munda.” Pamenepo Balaki mwana wa Zipori amene anali mfumu ya Mowabu nthaŵi imeneyo, adatuma amithenga kwa Balamu, mwana wa Beori, ku Petori, pafupi ndi mtsinje wa Yufurate m'dziko la kwao, kuti akamuitane ndi kumuuza kuti, “Anthu ochokera ku Ejipito adzaza dziko lonse, ndipo akuyang'anana ndi ine. Bwerani tsono muŵatemberere anthu ameneŵa m'malo mwanga, poti ngamphamvu kopambana ine. Mwina mwake ndidzatha kuŵagonjetsa ndi kuŵapirikitsa m'dziko mwanga. Pakuti ndikudziŵa kuti amene inu mumamdalitsa, amadalitsidwa, ndipo amene mumamtemberera, amatembereredwa.” Choncho akalonga a ku Mowabu ndi akalonga a ku Midiyani adanyamuka, atatenga ndalama m'manja zokaombedzera. Tsono adafika kwa Balamu namuuza mau a Balaki. Balamu adaŵauza kuti, “Gonani konkuno lero, ndipo ndikubwezerani mau monga momwe Chauta andiwuzire.” Choncho akalonga a ku Mowabu adagona kwa Balamu. Ndipo Mulungu adadza kwa Balamu namufunsa kuti, “Kodi anthu ali ndi iweŵa ndani?” Balamu adayankha kuti, “Balaki mwana wa Zipora mfumu ya Mowabu, watumiza uthenga kudzandiwuza kuti, ‘Anthu amene achokera ku Ejipito, adzaza dziko lonse. Bwerani tsono, muŵatemberere m'malo mwanga, mwina mwake ndidzatha kumenyana nawo nkhondo ndi kuŵapirikitsa.’ ” Apo Mulungu adauza Balamu kuti, “Usapite nao, ndipo usaŵatemberere anthuwo, chifukwa ngodalitsidwa.” Tsono Balamu adadzuka m'maŵa, naŵauza akalonga a Balaki aja kuti, “Bwererani ku dziko lakwanu, pakuti Chauta sadandilole kuti ndipite nanu.” Tsono akalonga a Mowabu aja adanyamuka napita kwa Balaki, ndipo adakamuuza kuti, “Balamu wakana kubwera.” Balaki adatumanso akalonga ochuluka ndi olemekezeka kopambana oyamba aja. Iwo adafika kwa Balamu namuuza kuti, “Balaki mwana wa Zipora akunena kuti, ‘Musalole kuti chinthu chilichonse chikuletseni kubwera kwa ine. Ndithudi, ndidzakuchitirani ulemu waukulu, ndipo chilichonse chimene mundiwuze, ndidzachita. Bwerani, mudzatemberere anthu ameneŵa m'malo mwanga.’ ” Koma Balamu adayankha atumiki a Balakiwo kuti, “Ngakhale Balaki akadati andipatse nyumba yake yodzaza ndi siliva ndi golide, sindikadatha kuchita zosiyana ndi zimene Chauta, Mulungu wanga, wandilamula. Sindikadatha kuchepetsa kapena kuwonjeza. Ndiye inu tsono, gonani konkuno usiku uno, monga adachitira anzanu aja, kuti ndidziŵe ngati pali zina zimene Chauta andiwuze.” Ndipo Mulungu adadza kwa Balamu usiku umenewo namuuza kuti, “Ngati anthuwo abwera kudzakuitana, nyamuka upite nao. Koma ukachite zokhazo zimene ndikakulamule.” Choncho Balamu, atadzuka m'maŵa mwake, adaika chishalo pa bulu wake, ndipo adanyamuka pamodzi ndi akalonga aja. Komabe Mulungu adapsa mtima chifukwa choti Balamuyo adapita. Ndipo mngelo wa Chauta adaimirira mu mseu, kuti amtsekere njira. Pamenepo nkuti atakwera bulu, ndipo ali ndi anyamata ake aŵiri. Bulu uja adaona mngelo wa Chauta ataima mu mseu, atasolola lupanga m'manja mwake. Tsono bulu adasiya mseu nakaloŵa m'munda. Apo Balamu adammenya bulu uja kuti abwerere mu mseu. Pambuyo pake mngelo wa Chauta uja adakaimirira m'kanjira kophaphatiza, kodzera pakati pa minda yamphesa, kokhala ndi khoma pa mbali zonse ziŵiri. Buluyo ataona mngelo wa Chauta, adadzipanikiza ku khoma, nakanikiza phazi la Balamu kukhomako. Pomwepo Balamu adamenya buluyo kachiŵiri. Kenaka mngelo wa Chauta adatsogolako nakaimiriranso pa malo ophaphatiza, opanda koti nkutembenukira kumanja kapena kumanzere. Buluyo ataona mngelo wa Chauta, adagona pansi, Balamu ali pamsana pake. Balamu adapsa mtima kwambiri, namenya buluyo ndi ndodo yake. Pamenepo Chauta adatsekula pakamwa pa buluyo, ndipo adalankhula, nafunsa Balamu kuti, “Kodi ndakuchitani chiyani kuti muzindimenya chotere katatu?” Balamu adauza buluyo kuti, “Chifukwa choti ukuseŵera nane, ndikadakhala ndi lupanga m'manja mwanga, ndikadakupha.” Buluyo adafunsanso Balamu kuti, “Kodi sindine bulu wanu amene mwakhala mukundikwera moyo wanu wonse mpaka lero lino? Kodi zimenezi ndidakuchitiranipo nkale lonse?” Balamu adayankha kuti “Iyai.” Pomwepo Chauta adatsekula maso a Balamu, ndipo adaona mngelo wa Chauta ataimirira m'njira, atasolola lupanga m'manja mwake. Tsono Balamu adazyolika, nadziponya pansi. Mngelo wa Chauta adamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani wamenya bulu wako chotere katatu? Ndabwera kudzakutsekera njira, chifukwa ulendo wakowu ukundiipira. Bulu wako anandiwona, ndipo anasiya njira katatu konse atandiwona. Akadapanda kusiya njira atandiwona, ndithu ndikadakuphera pomwepo, koma buluyo ndikadamleka kuti akhale moyo.” Balamu adayankha mngelo wa Chauta uja kuti, “Ndachimwa. Sindinalikudziŵa kuti mukunditsekera njira. Nchifukwa chake tsono, ngati zakuipirani, ndibwerera.” Apo mngelo wa Chauta adauza Balamu kuti, “Pita nawo anthuŵa. Koma ukanene zokhazo zimene ndikakuuze.” Choncho Balamu adapitirira ulendo wake pamodzi ndi akalonga a Balaki aja. Balaki atamva kuti Balamu wafika, adatuluka kukamchingamira ku mzinda wina wokhala pafupi ndi mtsinje wa Arinoni, umene umachita malire a dziko la Mowabu, kumapeto kwake kwenikweni. Ndipo Balaki adafunsa Balamu kuti, “Kodi sindidakutumireni mithenga yodzakuitanani? Chifukwa chiyani simudabwere? Kodi sindingathe kukuchitirani ulemu?” Balamu adayankha Balaki kuti, “Inde, ndabwera, koma kodi ndili ndi mphamvu zoti ndilankhule chinthu chilichonse? Ndiyenera kulankhula zokhazo zimene Mulungu andiwuze.” Tsono Balamu adapita limodzi ndi Balaki, nakafika ku Kiriyati-Huzoti. Kumeneko Balaki adapereka nsembe ya ng'ombe ndi nkhosa, natumizako nyama kwa Balamu ndi kwa akalonga amene anali naye aja. M'maŵa mwake Balaki adatenga Balamu, napita naye ku mapiri a Bamoti-Baala, kumene Balamuyo ankatha kuwona mahema onse a Aisraele mpaka ku mathero ake. Balamu adauza Balaki kuti, “Mundimangire maguwa asanu ndi aŵiri pano, ndipo mundikonzere ng'ombe zamphongo zisanu ndi ziŵiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziŵiri.” Balaki adachitadi monga momwe adamuuzira Balamu. Ndipo Balaki pamodzi ndi Balamu adapereka ng'ombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo pa guwa lililonse. Apo Balamu adauza Balaki kuti, “Imani pafupi ndi nsembe yanu yopsereza, tsono ine ndipite, mwina mwake Chauta abwera kudzakumana nane. Chilichonse chimene andiwonetse ndidzakuuzani.” Choncho adapita pamwamba pa phiri. Mulungu adakumana ndi Balamu, ndipo Balamuyo adati, “Ndakonza maguwa asanu ndi aŵiri, ndipo pa guwa lililonse ndaperekapo ng'ombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo.” Tsono Chauta adauza Balamu kuti “Bwerera kwa Balaki, ukamuuze izi! Izi” Balamu adabwerera kwa Balaki, nampeza iyeyo pamodzi ndi akalonga onse a Amowabu ataima pafupi ndi nsembe yake yopsereza. Apo Balamu adayamba kulankhula mau auneneri, adati, “Balaki mfumu ya ku Mowabu yandiitana kuchokera ku Aramu, ku mapiri akuvuma, kuti, ‘Bwerani, dzatemberereni Yakobe m'malo mwanga, bwerani mudzamfunire Israele zoipa.’ Koma ine ndingathe bwanji kumtemberera amene Mulungu sadamtemberere? Ndingathe bwanji kumufunira zoipa amene Chauta sadamfunire zoipa? Pamene ndikuŵaona kuchokera pamwamba pa phiri, pamene ndikuŵayang'ana kuchokera ku mapiri, ndikuwona anthu okhala paokha, osadziŵerengera kumodzi ndi mitundu ina. Ndani angathe kuŵerenga zidzukulu, zidzukulu za Yakobe zochuluka ngati fumbi, kapena kuŵerenga ngakhale chimodzi mwa zigawo zinai za fuko lonse la Israele? Lekeni ine ndife imfa ya anthu amene mudaŵalungamitsa, matsiriziro anga akhale onga a anthu amenewo.” Balaki adafunsa Balamu kuti, “Mwandichitira zotani? Suja ndidakuitanani kuti mudzatemberere adani anga, koma m'malo mwake mwangoŵadalitsa.” Iye adayankha kuti, “Kodi sindiyenera kulankhula zokhazo zimene Chauta adaika m'kamwa mwanga?” Balaki adamuuzanso kuti, “Tiyeni tipite limodzi ku malo ena kumene mungathe kuŵaona Aisraelewo. Mukangoona okhawo amene ayandikira pafupi, koma simukaona onse. Tsono muŵatemberere m'malo mwanga, mutaima pamenepo.” Adapita naye ku munda wa Zofimu pamwamba pa phiri la Pisiga, namangapo maguwa asanu ndi aŵiri, ndipo adapereka nsembe ya ng'ombe yamphongo ndi nsembe ya nkhosa yamphongo pa guwa lililonse. Balamu adauza Balaki kuti, “Imani pano pafupi ndi nsembe yanu yopsereza, ine ndipite ndikakumane ndi Chauta apo.” Chauta adakumana naye Balamu namuuza kuti, “Bwerera kwa Balaki, ndipo umuuze izi! Izi!” Tsono adabwerera kwa Balaki, ndipo adangoona akuimirira pafupi ndi nsembe yake yopsereza, ali ndi akalonga a ku Mowabu aja. Balaki adamufunsa kuti, “Nanga Chauta wakuuzani zotani?” Apo Balamu adayamba kulankhula mau auneneri, adati, “Dzukani, Balaki, ndipo mumve, mundimvere inu mwana wa Zipori. Mulungu sali ngati munthu kuti angathe kunama, si munthu kuti angathe kusintha maganizo ake. Kodi sadzachitadi zomwe adanena? Kapena sadzachitadi zimene adalankhula? Ndithu, ndalandira lamulo kuti ndidalitse. Iye wadalitsa, ndipo ine sindingathe kusintha kanthu. Iye sadaone choipa mwa Yakobe, sadaone chovuta mwa Israele. Chauta wao ali nawo, ndipo pakati pao pali kufuula kuti Iye ndi mfumu yao. Mulungu adaŵatulutsa m'dziko la Ejipito, ali ndi mphamvu zonga za njati. Zanyanga sizingamchite kanthu Yakobe, zamaula sizingathe kulimbana ndi Israele. Tsono anthu polankhula za Yakobe ndi za Israele adzati, ‘Onani zimene Mulungu wachita.’ Onani Aisraele, kudzuka kwanu kuli ngati kwa mkango waukazi, kudzambatuka kwanu kuli ngati kwa mkango waumuna, umene sugona pansi mpaka utagwira nyama ndi kuidya ndi kumwa magazi ake a nyama yojiwayo.” Balaki adauza Balamu kuti, “Musaŵatemberere, ndipo musaŵadalitse.” Koma Balamu adafunsa Balakiyo kuti, “Kodi sindidakuuzeni kuti ndiyenera kuchita zonse zimene Chauta wandiwuza?” Balaki adauza Balamu kuti, “Tiyeni limodzi tipite ku malo ena. Mwina mwake zidzamkondwetsa Mulungu kuti muŵatemberere m'malo mwanga, mutaima pamenepo.” Choncho Balaki adatenga Balamu, napita naye pamwamba pa phiri la Peori loyang'anana ndi chipululu cham'munsi. Tsono Balamu adauza Balaki kuti, “Mundimangire maguwa asanu ndi aŵiri pano, ndipo mundikonzere ng'ombe zamphongo zisanu ndi ziŵiri ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziŵiri.” Balaki adachitadi monga momwe adamuuzira Balamu, napereka ng'ombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo pa guwa lililonse. Pamene Balamu adaona kuti zinali zokondwetsa Chauta kuti adalitse Aisraele, sadapite monga nthaŵi zina zija kukafunsa kuti adziŵe zimene Mulungu akufuna, koma adangotembenuka nayang'ana ku chipululu. Adaona Aisraele ali m'mahema mwao, fuko lililonse pa lokha. Tsono mzimu wa Mulungu udatsika pa iye, ndipo adayamba kulankhula mau auneneri, adati, “Mau a Balamu mwana wa Beori, mau a munthu amene maso ake ndi otsekuka, munthu amene akumva mau a Mulungu, munthu amene akuwona Mphambe m'masomphenya, munthu amene akugwa pansi, koma maso ali chipenyere. Mahema ako, iwe Yakobe, nyumba zako, iwe Israele, si kukoma kwake! Anthu ako ali ngati zigwa zofika patali, ali ngati minda ya m'mbali mwa mtsinje, ali ngati khonje amene Chauta adabzala, ali ngati mitengo ya mkungudza yomera m'mbali mwa madzi. Madzi adzasefukira m'zotungira zao, ndipo mbeu zao zidzakhala ndi madzi ambiri, mfumu yao idzakhala yotchuka kupambana Agagi, ndipo ufumu wake udzakwezedwa. Mulungu adaŵatulutsa m'dziko la Ejipito. Ali ndi mphamvu zonga za njati, adzapha mitundu ya adani ao, adzaswa mafupa ao ndi kuŵaboola ndi mivi yao. Adamyata, nagona pansi ngati mkango ngati mkango wamphongo kapena waukazi. Kodi amuutse ndani? Ndi wodala munthu amene aŵadalitsa, ndi wotembereredwa munthu amene aŵatemberera.” Apo Balaki adapsera mtima Balamu, ndipo adaomba m'manja. Tsono Balakiyo adauza Balamu kuti, “Paja ndidakuitanani kuti mudzatemberere adani anga, ndipo inu mwaŵadalitsa katatu konseka. Nchifukwa chake, chokani, kazipitani kwanu. Ndidaakuuzani kuti ndidzakupatsani mphotho, koma Chauta wakana kuti muilandire mphothoyo.” Balamu adafunsa Balaki kuti “Kodi amithenga anu amene mudaŵatuma kwa ine aja, sindidaŵauze kuti, ‘Ngakhale Balaki andipatse nyumba yake yodzaza ndi siliva ndi golide, sindidzatha kuchita zosiyana ndi zimene Chauta wandiwuza. Sindidzachita zabwino kapena zoipa mwa kufuna kwanga. Ndidzalankhula zimene Chauta adzandiwuze?’ ” Balamu adauza Balaki kuti, “Tsopano ndikupita kwa anthu anga. Bwerani kuno, ndikudziŵitseni zimene Aisraeleŵa adzaŵachite anthu anu masiku akudzaŵa.” Ndipo adayambapo kulankhula mau auneneri adati, “Mau a Balamu mwana wa Beori, mau a munthu amene maso ake ndi otsekuka, munthu amene akumva mau a Mulungu, ndipo akudziŵa nzeru zake za Wopambanazonse, munthu amene akuwona Mphambe m'masomphenya, munthu amene akugwa pansi, koma maso ake ali chipenyere. Ndikupenya mtsogolo, ndipo ndikuona mtundu wa Israele. Mfumu yonga nyenyezi idzatuluka mwa Yakobe, ndodo yaufumu idzadzuka mwa Israele, idzatswanya atsogoleri a Mowabu, ndipo idzagonjetseratu mtundu wa Seti. Dziko la Edomu lidzalandidwa, Seiri mdani wake adzagonjetsedwa, pamene Aisraele adzakhala akupambanabe. Mwa Yakobe mudzatuluka mfumu yolamulira, imene idzaononga otsala mu mzinda.” Tsono Balamu adayang'ana Amaleke, ndipo adayamba kulankhula nati, “Mtundu wa Amaleke udaali wopambana mitundu ina yonse, koma potsiriza pake udzaonongeka.” Kenaka adayang'ana Akeni, tsono adayamba kulankhula nati, “Ngakhale malo amene mukukhalawo ngopanda zovuta, monga chisa chomangidwa pa thanthwe, komabe mudzaonongeka inu ana a Kaini, mudzakhala mu ukapolo wa Asuri nthaŵi yaitali.” Adayamba kulankhulanso nati, “Kalanga ine, ndani akhale moyo, Mulungu akachita zimenezi? Zombo zidzabwera kuchokera ku Kitimu, zidzaononga Asuri ndi Eberi. Kitimu nayenso adzaonongeka.” Tsono Balamu adanyamuka nabwerera kwao. Balaki nayenso adapita kwao. Pamene Aisraele anali ku Sitimu, anthu aamuna adayamba kuchita dama ndi akazi a ku Mowabu. Akaziwo ankaitana amuna ku nsembe za milungu yao, ndipo amunawo ankadya nawo, ndi kumapembedza milungu yaoyo. Choncho Aisraele adapembedza nao Baala wa ku Peori, ndipo Chauta adaŵapsera mtima Aisraele. Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Utenge atsogoleri onse a Aisraele ndipo uŵanyonge poyera pamaso panga, kuti ndileke kukwiyira Israele.” Apo Mose adauza oweruza a Aisraele kuti, “Aliyense mwa inu aphe anthu ake amene adapembedza nao Baala wa ku Peori.” Tsono Mwisraele wina adabwera ndi mkazi Wachimidiyani kubanja kwake, Mose ndi Aisraele onse akupenya, pamene ankalira pakhomo pa chihema chamsonkhano. Finehasi mwana wa Eleazara, mdzukulu wa Aroni, ataona zimenezo, adadzuka nasiya mpingowo, nakatenga mkondo. Ndipo adatsatira Mwisraele uja mpaka kukaloŵa m'chipinda cham'kati, nabaya onse aŵiriwo, Mwisraeleyo pamodzi ndi mkaziyo. Motero mliri udaleka pakati pa Aisraele. Komabe anthu okwanira 24,000 anali atafa kale ndi mliriwo. Chauta adauza Mose kuti, “Finehasi mwana wa Eleazara, mdzukulu wa Aroni, wandiletsa kuti ndisaŵaononge Aisraele, chifukwa choti sadalole kuti wina aliyense apembedze mulungu wina koma Ine, nchifukwa chake sindidaŵaononge ndili wokwiya. Motero umuuze kuti ndikupangana naye tsopano chipangano chamtendere. Ndikupangana naye iyeyu ndi zidzukulu zake zonse, chipangano cha unsembe wamuyaya, chifukwa sadalole kuti anthu aukire Ine Mulungu, ndipo adachita ntchito yopepesera machimo a Aisraele.” Mwisraele amene adaphedwa pamodzi ndi mkazi Wachimidiyani uja anali Zimiri mwana wa Salu, mtsogoleri wa banja la makolo a Asimeoni. Ndipo mkazi Wachimidiyani amene adaphedwayo anali Kozibi mwana wa Zuri, amene anali mtsogoleri wa mbumba ina ya fuko la ku Midiyani. Chauta adauza Mose kuti, “Uŵathire nkhondo Amidiyani, ndiponso uŵaononge chifukwa choti adakuchitani zachabe pokunyengani ku Peori, ndiponso chifukwa cha nkhani ya mlongo wao Kozibi, mwana wamkazi wa mfumu ya ku Midiyani, amene adaphedwa pa nthaŵi ya mliri chifukwa cha zochitika ku Peori zija.” Utatha mliriwo, Chauta adauza Mose ndi Eleazara, mwana wa wansembe Aroni, kuti, “Uchite chiŵerengero cha mpingo wonse wa Aisraele, kuyambira anthu aamuna a zaka makumi aŵiri ndi opitirirapo, potsata mabanja a makolo ao, anthu onse a m'dziko la Israele amene angathe kumenya nkhondo.” Tsono Mose ndi wansembe Eleazara adalankhula ndi atsogoleri m'zigwa za ku Mowabu, pafupi ndi mtsinje wa Yordani ku Yeriko, adati, “Muchite chiŵerengero cha anthu, kuyambira a zaka makumi aŵiri ndi opitirirapo,” monga momwe Chauta adaalamulira Mose. Aisraele amene adatuluka m'dziko la Ejipito anali aŵa: Fuko la Rubeni. Rubeni anali mwana wachisamba wa Israele. Ana aamuna a Rubeni anali aŵa: Hanoki anali kholo la banja la Ahanoki. Palu anali kholo la banja la Apalu. Hezironi anali kholo la banja la Ahezironi. Karimi anali kholo la banja la Akarimi. Ameneŵa, anthu okwanira 43,730, ndiwo anali a m'mabanja a Rubeni, amene adaŵerengedwa. Mwana wa Palu anali Eliyabu, ndipo ana a Eliyabu anali Nemuwele, Datani ndi Abiramu. Ameneŵa anali omwe aja amene adasankhidwa mu mpingo, amenenso adakangana ndi Mose ndi Aroni pogwirizana ndi Kora, pamene adatsutsana ndi Chauta. Ndipo nthaka idang'ambika ndi kuŵameza onsewo pamodzi ndi Kora, kotero kuti gulu lao lidafa pamene moto udapsereza anthu 250 aja, nasanduka chenjezo. Komabe a m'banja la Kora sadafe onse. Ana aamuna a Simeoni potsata mabanja ao ana aamuna a Simeoni anali aŵa: Nemuwele anali kholo la banja la Anemuele. Yamini anali kholo la banja la Ayamini. Yakini anali kholo la banja la Ayakini. Zera anali kholo la banja la Azera. Shaulo anali kholo la banja la Ashaulo. Ameneŵa, anthu okwanira 22,200, ndiwo a m'mabanja a Simeoni, amene adaŵerengedwa. Potsata mabanja ao ana aamuna a Gadi anali aŵa: Zefoni anali kholo la banja la Azefoni. Hagi anali kholo la banja la Ahagi. Suni anali kholo la banja la Asuni. Ozini anali kholo la banja la Aozini. Eri anali kholo la banja la Aeri. Arodi anali kholo la banja la Aarodi. Areli anali kholo la banja la Aareli. Ameneŵa, anthu okwanira 40,500, ndiwo anali a m'mabanja a Gadi, amene adaŵerengedwa. Ana aamuna a Yuda anali Ere ndi Onani, koma iwowo adafera m'dziko la Kanani. Potsata mabanja ao ana ena aamuna a Yuda anali aŵa: Sela anali kholo la banja la Asela. Perezi anali kholo la banja la Aperezi. Zera anali kholo la Azera. Tsono ana aamuna a Perezi anali aŵa: Hezironi anali kholo la banja la Ahezironi. Hamuli anali kholo la banja la Ahamuli. Ameneŵa, anthu okwanira 76,500, ndiwo anali a m'mabanja a Yuda, amene adaŵerengedwa. Potsata mabanja ao ana aamuna a Isakara anali aŵa: Tola anali kholo la banja la Atola. Puva anali kholo la banja la Apuva. Yasubu anali kholo la banja la Ayasubu. Simeoni anali kholo la banja la Asimeoni. Ameneŵa, anthu okwanira 64,300, ndiwo anali a m'mabanja a Isakara, amene adaŵerengedwa. Potsata mabanja ao ana aamuna a Zebuloni anali aŵa: Seredi anali kholo la banja la Aseredi. Eloni anali kholo la banja la Aeloni. Yaleele anali kholo la banja la Ayaleele. Ameneŵa, anthu okwanira 60,500, ndiwo anali a m'mabanja a Zebuloni, amene adaŵerengedwa. Potsata mabanja ao ana aamuna a Yosefe anali aŵa: Manase ndi Efuremu. Ana aamuna a Manase anali aŵa: Makiri anali kholo la banja la Amakiri. Makiri anali bambo wa Giliyadi. Giliyadi anali kholo la banja la Agiliyadi. Ana aamuna a Giliyadi anali aŵa: Iyezere anali kholo la banja la Aiyezere. Heleki anali kholo la banja la Aheleki. Ndipo Asiriele anali kholo la banja la Aasiriele. Sekemu anali kholo la banja la Asekemu. Semida anali kholo la banja la Asemida. Hefere anali kholo la banja la Ahefere. Koma Zelofehadi mwana wa Hefere analibe ana aamuna, koma ana aakazi okhaokha. Ana aakazi a Zelofehadi anali aŵa: Mala, Nowa, Hogola, Milika ndi Tiriza. Ameneŵa, anthu okwanira 52,700, ndiwo anali a mabanja a Manase, amene adaŵerengedwa. Potsata mabanja ao ana aamuna a Efuremu anali aŵa: Sutela anali kholo la banja la Asutela, Bekeri anali kholo la banja la Abekeri. Tahani anali kholo la banja la Atahani. Ndipo ana aamuna a Sutela anali aŵa: Erani anali kholo la banja la Aerani. Ameneŵa, anthu okwanira 32,500, ndiwo adaŵerengedwa pa mabanja a ana aamuna a Efuremu, zidzukulu za Yosefe potsata mabanja ao. Potsata mabanja ao ana aamuna a Benjamini anali aŵa: Bela anali kholo la banja la Abela. Asibele anali kholo la banja la Aasibele. Ahiramu anali kholo la banja la Aahiramu. Sefufamu anali kholo la banja la Asefufamu. Hafamu anali kholo la banja la Ahufamu. Ndipo ana aamuna a Bela anali Aradi ndi Namani. Aradi anali kholo la banja la Aaradi. Namani anali kholo la banja la Anamani. Ameneŵa, anthu okwanira 45,600, ndiwo anali a m'mabanja a Benjamini, amene adaŵerengedwa. Potsata mabanja ao ana aamuna a Dani anali aŵa: Suhamu anali kholo la banja la Asuhamu. Ameneŵa ndiwo mabanja a Dani potsata mabanja ao. Anthu oŵerengedwa pa mabanja onse a Suhamu adakwanira 64,400. Potsata mabanja ao ana aamuna a Asere anali aŵa: Imina, anali kholo la banja la Aimina. Isivi anali kholo la banja la Aisivi. Beriya anali kholo la banja la Aberiya. Ana aamuna a Beriya anali aŵa: Hebere anali kholo la banja la Ahebri. Malikiele anali kholo la banja la Amalikiele. Mwana wamkazi wa Asere anali Sera. Ameneŵa, anthu okwanira 53,400, ndiwo adaŵerengedwa pa mabanja a Asere. Potsata mabanja ao ana aamuna a Nafutali anali aŵa: Yazeele anali kholo la banja la Ayazeele. Guni anali kholo la banja la Aguni. Yezere anali kholo la banja la Ayezere. Silemu anali kholo la banja la Asilemu. Ameneŵa, anthu okwanira 45,400, ndiwo adaŵerengedwa pa mabanja a Nafutali. Chiŵerengero chonse cha Aisraele chinali 601,730. Chauta adauza Mose kuti, “Uŵagaŵire dziko anthu ameneŵa, kuti likhale choloŵa chao, molingana ndi chiŵerengero cha maina ao. Fuko lalikulu ulipatse choloŵa chachikulu, fuko laling'ono choloŵa chaching'ono. Fuko lililonse lilandire choloŵa chake molingana ndi chiŵerengero cha anthu ake. Koma dzikolo uligaŵe mwamaere. Alandire choloŵa chao potsata kuchuluka kwa maina a mafuko a makolo ao. Choloŵa chaocho, uchigaŵe pakati pa fuko lalikulu ndi laling'ono mwamaere.” Potsata mabanja ao chiŵerengero cha Alevi chinali motere: Geresoni anali kholo la banja la Ageresoni. Kohati anali kholo la banja la Akohati. Merari anali kholo la banja la Amerari. Mabanja a Alevi anali aŵa: banja la Alibini, banja la Ahebroni, banja la Amahali, banja la Amusi, banja la Akora. Kohati anali bambo wa Amuramu. Mkazi wa Amuramu anali Yokebede mwana wa Levi, amene adabadwira ku Ejipito. Yokebedeyo adamubalira Amuramu ana aŵa: Aroni, Mose ndi Miriyamu mlongo wao. Aroni adabala Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara. Koma Nadabu ndi Abihu adafa chifukwa adaapereka moto wosaloledwa pamaso pa Chauta. Onse amene adaŵerengedwa mwa Aleviwo anali 23,000, kuyambira ana aamuna a mwezi umodzi ndi opitirirapo. Iwowo sadaŵaŵerengere kumodzi ndi Aisraele, chifukwa sadapatsidwe choloŵa pakati pa Aisraele. Ameneŵa ndiwo anthu amene adaŵerengedwa ndi Mose ndi wansembe Eleazara. Iwowo adaŵerenga Aisraelewo ku zigwa za Mowabu, pafupi ndi mtsinje wa Yordani, ku Yeriko. Koma pakati pa anthu ameneŵa panalibe ndi mmodzi yemwe wamoyo amene adaaŵerengedwa kale ndi Mose ndi wansembe Aroni, pamene ankaŵerenga Aisraelewo ku chipululu cha Sinai. Paja za iwowo Chauta adati, “Adzafera m'chipululu.” Sadatsale ndi mmodzi yemwe mwa iwo, kupatula Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni. Nthaŵi imeneyo kudabwera ana aakazi a Zelofehadi. Iyeyo anali mwana wa Hefere, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase, a m'mabanja a Manase mwana wa Yosefe. Ana ake aakaziwo anali aŵa: Mala, Nowa, Hogola, Milika ndi Tiriza. Iwoŵa adakaima pamaso pa Mose, pa wansembe Eleazara, pa atsogoleri, ndiponso pamaso pa mpingo wonse, pakhomo pa chihema chamsonkhano, nati, “Bambo wathu adafera m'chipululu. Iyeyo sanali nao m'gulu la anthu aja amene adasonkhana pamodzi ndi Kora naukira Chauta, iye adafera tchimo lake, koma analibe ana aamuna. Kodi dzina la bambo wathu life chifukwa choti analibe mwana wamwamuna? Mutipatse choloŵa chathu pakati pa abale a bambo wathu.” Mose adapita ndi mlandu umenewu pamaso pa Chauta. Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Ana aakazi a Zelofehadiwo akunena zoona. Uŵapatse choloŵa chao pakati pa abale a bambo wao. Uŵapatse choloŵa cha bambo waocho kuti chikhale chao. Ndipo uŵauze Aisraele kuti, ‘Munthu akafa opanda mwana wamwamuna, choloŵa chake chikhale cha mwana wake wamkazi. Akakhala kuti alibe mwana wamkazi, choloŵa chakecho chikhale cha abale ake. Akakhala kuti alibe abale, choloŵa chakecho chikhale cha abale a bambo wake. Bambo wakeyo akakhala wopanda abale, choloŵa chakecho upatse wachibale wake pabanja pakepo, ndipo chidzakhala chake. Ameneŵa akhale malamulo ndi malangizo kwa Aisraele, monga momwe Chauta adaalamulira Mose.’ ” Chauta adauza Mose kuti, “Ukwere phiri ili la Abarimu, kuti uwone dziko limene ndapatsa Aisraele. Ndipo utaliwona, udzamwalira monga momwe adachitira Aroni mbale wako, chifukwa simudamvere mau anga m'chipululu cha Zini pa nthaŵi imene mpingo udandiwukira ku madzi a Meriba, pamene simudaonetse kuyera kwanga pamaso pao.” (Ameneŵa ndiwo madzi a kasupe wa ku Meriba ku Kadesi, m'chipululu cha Zini.) Mose adapempha Chauta kuti, “Inu Chauta, mwini mpweya wopatsa moyo anthu onse, musankhe munthu kuti aziyang'anira mpingowu. Munthuyo aziŵatsogolera pa nkhondo ndi kuŵalamula, kuti mpingo wanu usamakhale ngati nkhosa zopanda mbusa.” Apo Chauta adauza Mose kuti, “Tenga Yoswa mwana wa Nuni, munthu amene mzimu wa Mulungu uli mwa iye, ndipo umsanjike manja. Umuimiritse pamaso pa wansembe Eleazara ndi pamaso pa mpingo wonse, tsono umlonge m'malo mwako, iwo akupenya. Umpatseko udindo wako, kuti mpingo wonse wa Aisraele uzimumvera. Tsono adzapite kwa wansembe Eleazara amene adzamdziŵitse zimene Chauta akufuna, pofunsa kwa Urimu ndi Tumimu. Umotu ndi m'mene Iyeyu adzatsogolere ndi kulamula Yoswa ndi mpingo wonse wa Aisraele.” Mose adachitadi monga momwe Chauta adamlamulira. Adamtengadi Yoswa namuimiritsa pamaso pa wansembe Eleazara ndi pamaso pa mpingo wonse. Ndipo adamsanjika manja, nampatsa udindo monga momwe Chauta adamlangizira kudzera mwa Mose. Chauta adauza Mose kuti, “Lamula Aisraele, ndipo uŵauze kuti, ‘Muzisamala kupereka kwa Ine pa nthaŵi yake zopereka zanga, chakudya changa cha nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo londikomera.’ Ndipo uŵauzenso kuti, nsembe yotentha pa moto, yoti muzipereka kwa Chauta ndi iyi: Muzipereka anaankhosa aŵiri amphongo a chaka chimodzi opanda chilema, tsiku ndi tsiku, kuti akhale nsembe yosalekeza. Mwanawankhosa mmodzi muzimpereka m'maŵa, winayo muzimpereka madzulo. Muziperekanso kilogaramu limodzi la ufa wosalala, wosakaniza ndi mafuta aolivi oyenga bwino okwanira lita limodzi. Imeneyi ndiyo nsembe yopsereza imene idalamulidwa pa phiri la Sinai, kuti itulutse fungo lokoma, nsembe yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta. Chopereka cha chakumwa pa nkhosa iliyonse chikhale yokwanira lita limodzi. Muzithira vinyo waukaliyo m'malo opatulika, kuchipereka kwa Chauta. Mwanawankhosa wina uja muzimpereka madzulo, pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa zonga zam'maŵa zija. Imeneyi ikhalenso nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta. “Pa tsiku la Sabata muzipereka anaankhosa aŵiri amphongo a chaka chimodzi opanda chilema. Muziperekanso makilogaramu aŵiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta ngati chopereka cha chakudya, ndipo muziperekanso chopereka cha chakumwa. Imeneyo ndiyo nsembe yopsereza ya tsiku la Sabata lililonse, kuwonjezera pa nsembe zopsereza ndi pa zopereka za chakumwa za tsiku ndi tsiku zija. “Pa tsiku loyamba la mwezi uliwonse, muzipereka nsembe yopsereza kwa Chauta. Nsembeyo ikhale ya anaang'ombe aŵiri amphongo, nkhosa imodzi yamphongo, anaankhosa asanu ndi aŵiri amphongo a chaka chimodzi, opanda chilema. Chopereka cha chakudya ikhale ya ufa wosalala wa makilogaramu atatu, wosakaniza ndi mafuta, pa ng'ombe yamphongo iliyonse. Muperekenso makilogaramu aŵiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, pa nkhosa yamphongoyo, ndiponso kilogaramu limodzi la ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, pa mwanawankhosa aliyense. Imeneyo ndiyo nsembe yopsereza yotulutsa fungo lokoma, nsembe yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta. Chopereka cha chakumwa chikhale cha vinyo wokwanira malita aŵiri pa ng'ombe yamphongo iliyonse, ya vinyo wokwanira lita limodzi ndi theka pa nkhosa yamphongoyo, ndi ya vinyo wokwanira lita limodzi pa mwanawankhosa aliyense. Imeneyi ndiyo nsembe yopsereza ya mwezi uliwonse, pa miyezi yonse ya chaka. Aperekenso tonde kuti akhale nsembe yopepesera machimo, yopereka kwa Chauta. Aipereke kuwonjezera pa nsembe zopsereza ndi zopereka za zakumwa za tsiku ndi tsiku. “Tsiku la 14 la mwezi woyamba, ndi la Paska ya Chauta. Ndipo pa tsiku la 15 la mwezi umenewu, ndi tsiku lachikondwerero. Azidya buledi wosafufumitsa masiku asanu ndi aŵiri. Pa tsiku loyamba pazikhala msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito yotopetsa, koma mupereke nsembe yotentha pa moto, nsembe yopsereza ya Chauta. Ikhale ya anaang'ombe aŵiri amphongo, nkhosa yamphongo imodzi ndi anaankhosa asanu ndi aŵiri a chaka chimodzi, opanda chilema. Muperekenso chopereka cha chakudya wosakaniza ndi mafuta. Ufa wake ukhale wa makilogaramu atatu pa ng'ombe yamphongo iliyonse, wa makilogaramu aŵiri pa nkhosa yamphongoyo, ndiponso wa makilogaramu limodzi pa mwanawankhosa aliyense. Muperekenso tonde mmodzi kuti akhale nsembe yochitira mwambo wopepesera machimo anu. Muzipereka zimenezi kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zopereka nthaŵi yam'maŵa. Motero pa masiku asanu ndi aŵiri muzipereka tsiku lililonse chakudya cha nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta. Muchipereke kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija pamodzi ndi zopereka za chakumwa. Ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri muchite msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito zotopetsa. “Pa tsiku la zipatso zoyambirira kucha, pamene mukupereka chopereka cha chakudya chatsopano kwa Chauta, pa tsiku la chikondwerero cha masabata, muchite msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito zotopetsa, koma mupereke nsembe yopsereza, yotulutsa fungo lokomera Chauta. Ikhale ya anaang'ombe aŵiri amphongo, nkhosa imodzi yamphongo, ndi anaankhosa asanu ndi aŵiri amphongo a chaka chimodzi. Muperekenso chopereka cha chakudya wosakaniza ndi mafuta, wa makilogaramu atatu pa ng'ombe yamphongo iliyonse, wa makilogaramu aŵiri pa nkhosa yamphongoyo, ndiponso wa kilogaramu limodzi pa mwanawankhosa aliyense. Muperekenso tonde mmodzi wochitira mwambo wopepesera machimo anu. Mupereke zimenezi pamodzi ndi zopereka za chakumwa, kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija ndi chopereka cha chakudya. Musamale kuti nyamazo zikhale zopanda chilema. “Pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiŵiri, muzichita msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito zotopetsa. Tsiku limeneli muziliza malipenga. Ndipo mupereke nsembe yopsereza, yotulutsa fungo lokomera Chauta. Ikhale ya mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa imodzi yamphongo, anaankhosa asanu ndi aŵiri amphongo a chaka chimodzi, opanda chilema. Muperekenso chopereka cha chakudya chosakaniza ndi mafuta, wa makilogaramu atatu pa ng'ombe yamphongo iliyonse, wa makilogaramu aŵiri pa nkhosa yamphongoyo, ndiponso wa kilogaramu limodzi pa mwanawankhosa aliyense. Muperekenso tonde mmodzi kuti akhale nsembe yochitira mwambo wopepesera machimo anu. Mupereke zonsezi kuwonjezera pa nsembe yopsereza yopereka mwezi ukakhala, pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya, kuwonjezeranso pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija, pamodzi ndi nsembe zaufa ndi zopereka za chakumwa, potsata malamulo ake, kuti zitulutse fungo lokoma, nsembe zotentha pa moto, zopereka kwa Chauta. “Pa tsiku lakhumi la mwezi wachisanu ndi chiŵiri womwewo, muchite msonkhano wopatulika, ndipo musale zakudya. Musagwire ntchito iliyonse, koma mupereke kwa Chauta nsembe yopsereza, yotulutsa fungo lokoma. Ikhale ya mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa imodzi yamphongo, ndi anaankhosa asanu ndi aŵiri amphongo a chaka chimodzi. Musankhule nyama zopanda chilema. Ndipo mupereke chopereka cha chakudya chosakaniza ndi mafuta, wa makilogaramu atatu pa ng'ombe yamphongoyo, wa makilogaramu aŵiri pa nkhosa yamphongoyo, ndiponso wa kilogaramu limodzi pa mwanawankhosa aliyense. Muperekenso tonde mmodzi kuti akhale nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe yopepesera machimo ya pa tsiku la mwambo wopepesera machimo, kuwonjezeranso pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija, pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa.” “Pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiŵiri womwewo, muchite msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito zotopetsa, ndipo muchite chikondwerero cholemekeza Chauta masiku asanu ndi aŵiri. Pa tsiku loyamba mupereke nsembe yopsereza, nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta. Ikhale ya anaang'ombe khumi ndi atatu amphongo, nkhosa ziŵiri zamphongo, anaankhosa khumi ndi anai amphongo a chaka chimodzi. Nyama zonsezo zikhale zopanda chilema. Muperekenso choperaka cha chakudya chosakaniza ndi mafuta, wa makilogaramu atatu pa ng'ombe yamphongo iliyonse, wa makilogaramu aŵiri pa nkhosa yamphongo iliyonse, ndi wa kilogaramu limodzi pa mwanawankhosa aliyense. Muperekenso tonde mmodzi kuti akhale nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija, pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa. “Pa tsiku lachiŵiri mupereke anaang'ombe khumi ndi aŵiri amphongo, nkhosa ziŵiri zamphongo, anaankhosa khumi ndi anai amphongo a chaka chimodzi opanda chilema, pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa pa ng'ombe zamphongo zija, pa nkhosa zamphongo zija, ndi pa anaankhosa aja, malinga ndi chiŵerengero cha nyamazo ndi potsata malangizo ake. Muperekenso tonde mmodzi kuti akhale nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija, pamodzi ndi zopereka za chakudya ndi za zakumwa. “Pa tsiku lachitatu mupereke ng'ombe zamphongo khumi ndi imodzi, nkhosa ziŵiri zamphongo, anaankhosa khumi ndi anai amphongo, a chaka chimodzi, opanda chilema, pamodzi ndi zopereka zake zachakudya ndi za chakumwa pa ng'ombe zamphongo zija, pa nkhosa zamphongo zija, ndi pa anaankhosa aja, molingana ndi chiŵerengero cha nyamazo ndi potsata malangizo ake. Muperekenso tonde mmodzi kuti akhale yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku zija, pamodzi ndi zopereka zachakudya ndi za chakumwa. “Pa tsiku lachinai mupereke ng'ombe khumi zamphongo, nkhosa ziŵiri zamphongo, anaankhosa amphongo khumi ndi anai a chaka chimodzi opanda chilema, pamodzi ndi zopereka zake zachakudya ndi za chakumwa pa ng'ombe zija, pa nkhosa zija, ndi pa anaankhosa aja, molingana ndi chiŵerengero cha nyamazo ndi potsata malangizo ake. Muperekenso tonde mmodzi kuti akhale nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija, pamodzi ndi zopereka zake zachakudya ndi za chakumwa. “Pa tsiku lachisanu mupereke ng'ombe zisanu ndi zinai zamphongo, nkhosa ziŵiri zamphongo, anaankhosa khumi ndi anai amphongo a chaka chimodzi opanda chilema, pamodzi ndi zopereka zake zachakudya ndi za chakumwa pa ng'ombe zija, pa nkhosa zija, ndi pa anaankhosa aja, molingana ndi chiŵerengero cha nyamazo ndi potsata malangizo ake. Muperekenso tonde mmodzi kuti akhale nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija, pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.” “Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi mupereke ng'ombe zisanu ndi zitatu zamphongo, nkhosa ziŵiri zamphongo, anaankhosa khumi ndi anai amphongo a chaka chimodzi opanda chilema, pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa pa ng'ombe zamphongo zija, pa nkhosa zamphongo zija, ndi pa anaankhosa aja, molingana ndi chiŵerengero cha nyamazo ndi potsata malangizo ake. Muperekenso tonde mmodzi kuti akhale nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija, pamodzi ndi zopereka zake za chakudya ndi za chakumwa. “Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri mupereke ng'ombe zisanu ndi ziŵiri zamphongo, nkhosa ziŵiri zamphongo, anaankhosa khumi ndi anai amphongo a chaka chimodzi opanda chilema. Muperekenso chopereka cha zakudya ndi zachakumwa pa ng'ombe zamphongo zija, pa nkhosa zamphongo zija, ndi pa anaankhosa aja, molingana ndi chiŵerengero cha nyamazo ndi potsata malangizo ake. Muperekenso tonde mmodzi kuti akhale nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija, pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi zachakumwa.” “Pa tsiku lachisanu ndi chitatu muchite msonkhano waulemu. Musagwire ntchito zotopetsa, koma mupereke nsembe yopsereza, nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta. Ikhale ya ng'ombe imodzi yamphongo, nkhosa imodzi yamphongo, anaankhosa asanu ndi aŵiri amphongo a chaka chimodzi opanda chilema. Ndipo mupereke chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa pa ng'ombe yamphongo ija, pa nkhosa yamphongo ija, ndi pa anaankhosa aja, molingana ndi chiŵerengero cha nyamazo ndi potsata malangizo ake. Muperekenso tonde mmodzi kuti akhale nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija, pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa. “Zimenezi ndizo zimene mudzapereke kwa Chauta pa masiku osankhidwa achikondwerero, kuwonjezera pa zopereka zanu zimene mudazilumbirira ndi pa zopereka zanu zaufulu: nsembe zanu zopsereza, nsembe zanu zaufa, nsembe zanu zachakumwa ndi nsembe zanu zachiyanjano.” Tsono Mose adauza Aisraele zonse, monga momwe Chauta adaamlamulira. Mose adauza atsogoleri a mafuko a Aisraele kuti, Chauta walamula kuti, “Pamene munthu wamwamuna alumbira kwa Chauta kapena alonjeza kuti adzachitadi zimene walumbira, asaphwanye lonjezo lakelo. Achite molingana ndi zimene adalumbira. Mkazi akakhala mtsikana, nakhalabe m'nyumba ya bambo wake, ndipo alumbira kwa Chauta kuti adzachitadi zina zake zimene walumbira, tsono bambo wake nkumva za kulumbira kwakeko ndi za malonjezo amene walumbira kuti adzachitadi, koma bambo wakeyo osalankhula kanthu, mwanayo achitedi zimene adalumbirazo. Ayenera kuchitadi zonse zimene walonjezazo. Koma bambo wake akamkaniza mwanayo pa tsiku lomwe wamva zimenezo, palibe lamulo lomkakamiza mwanayo kuti achite zimene adalumbirazo ndi zimene adalonjezazo. Chauta adzamkhululukira mwanayo chifukwa choti bambo wake adamkaniza. Ngati mkazi alonjeza kapena alumbira mosaganiza bwino kuti adzachitadi kanthu kena, ndipo pambuyo pake akwatiwa, tsono mwamuna wake nkumva, koma osamuuza kanthu mkaziyo pa tsiku lomwe wamvalo, mkaziyo achitedi zimene walumbirazo, achite ndithu zimene walonjezazo. Koma ngati pa tsiku limene mwamunayo wamva zimenezo, amkaniza, pamenepo ammasula mkaziyo kwa zimene adalumbira ndi kwa zimene adalankhula mosaganiza bwino, ndipo Chauta adzamkhululukira. “Mkazi wamasiye kapena wosudzulidwa akalumbira kapena kulonjeza kuti adzachita kanthu kalikonse, ayenera kukachitadi. “Mkazi wokwatiwa akalonjeza nalumbira kuti adzachitadi zimene walonjeza, tsono mwamuna wake nkumva, koma osamuuza kanthu mkaziyo ndiponso osamkaniza, ayenera kuchitadi zonse zimene adalumbira ndi zonse zimene adalonjeza. Koma pa tsiku limene mwamuna wake wamva zimenezo, akamletsa mkaziyo kuti asachite zimene adalumbirazo, palibe lamulo lomkakamiza mkaziyo kuchita zimene adalumbira kapenanso zimene adalonjeza. Mwamuna wake waletsa, ndipo Chauta adzamkhululukira mkaziyo. Mwamuna wake ali ndi mphamvu za kuvomereza kapena kukana zimene mkaziyo adalumbira kapena zimene adalonjeza zokhudza za kudzilanga. Koma ngati m'maŵa mwake ndi masiku otsatirawo mwamuna wake samkaniza, atamva zimenezo, mkaziyo achitedi zonse zimene adalumbira, kapena zimene adalonjeza. Mwamunayo wavomereza zimenezo, chifukwa choti sadamuuze kanthu mkaziyo pa tsiku limene adamva. Koma mwamunayo akamkaniza patapita kanthaŵi atazimva kale, iyeyo ndiye wochimwa pamalo pa mkaziyo.” Ameneŵa ndiwo malamulo amene Chauta adalamula Mose za mwamuna ndi mkazi wake, ndiponso za bambo ndi mwana wake wamkazi amene akadali mtsikana wokhalabe m'nyumba ya bambo wake. Chauta adauza Mose kuti, “Ulipsire Amidiyani chifukwa cha zimene adachitira Aisraele, tsono pambuyo pake udzafa.” Mose adauza Aisraele kuti, “Amuna ena pakati panupa mutenge zida zankhondo, kuti mukamenyane ndi Amidiyani, kuti Chauta aŵalipsire. Mutumize ku nkhondo anthu chikwi chimodzi pa fuko lililonse la Israele.” Choncho pa anthu a Aisraele ambirimbiri aja, Mose adatumiza anthu chikwi chimodzi pa fuko lililonse, ndipo onse anali 12,000 pamodzi. Mose adaŵatumiza ku nkhondo anthuwo, chikwi chimodzi pa fuko lililonse, pamodzi ndi Finehasi mwana wa wansembe Eleazara, iyeyu atanyamula zipangizo za ku malo opatulika ndi malipenga ochenjeza m'manja mwake. Aisraelewo adamenyana nkhondo ndi Amidiyani, monga momwe Chauta adaalamulira Mose, ndipo adapha amuna onse. Adapha mafumu a ku Midiyani pamodzi ndi anthu ao omwe. Mafumuwo anali Evi, Rekemu, Zuri, Huri ndi Reba, mafumu asanu a ku Midiyani. Adaphanso ndi lupanga Balamu mwana wa Beori. Ndipo adagwira akazi a ku Midiyani ukapolo, pamodzi ndi ana ao. Adalandanso ng'ombe zao, nkhosa zao, ndi chuma chao chonse. Adatentha mizinda yonse imene iwo ankakhalamo, ndi zithando zao zonse, natenga zonse zimene adalanda kunkhondoko, anthu pamodzi ndi nyama zomwe. Tsono adabwera nawo akapolowo, pamodzi ndi zonse zimene adalandazo, kwa Mose, kwa wansembe Eleazara ndi kwa mpingo wonse wa Aisraele, ku zithando za ku zigwa za Mowabu, pafupi ndi mtsinje wa Yordani ku Yeriko. Mose ndi wansembe Eleazara, pamodzi ndi atsogoleri a mpingo, adakaŵachingamira kunja kwa zithando. Ndipo Mose adakwiyira akulu ankhondowo, atsogoleri olamulira ankhondo zikwi ndiponso atsogoleri olamulira ankhondo mazana, amene ankachokera ku nkhondo. Mose adaŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mwaŵasiya amoyo akazi onse? Paja akazi ameneŵa adatsata uphungu wa Balamu, nasokeretsa Aisraele kuti asachitenso zokhulupirika pamaso pa Chauta ku Peori kuja, kotero kuti mliri udagwera mpingo wa Chauta. Nchifukwa chake tsono iphani mwana wamwamuna aliyense, ndi mkazi aliyense amene adadziŵapo ndi mwamuna. Koma atsikana amene sadagone ndi mwamuna, muŵasunge akhale anu. Tsono aliyense mwa inu amene wapha munthu, kapena amene wakhudza mtembo, akhale kunja kwa mahema masiku asanu ndi aŵiri. Pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, mudziyeretse inuyo pamodzi ndi akapolo anu. Muyeretse chovala chilichonse, chinthu chilichonse chachikopa, chinthu chilichonse chopangidwa ndi ubweya wambuzi, ndi chinthu chilichonse chopangidwa ndi mtengo.” Tsono wansembe Eleazara adauza ankhondo amene adaapita ku nkhondowo kuti, “Lamulo limene Chauta walamula Mose ndi ili: Izi zokha, golide, siliva, mkuŵa, chitsulo, chiwaya ndi mtovu, zonse zimene sizingathe kupsa ndi moto, muziike pa moto, ndipo zidzayeretsedwa. Komabe ziyeretsedwenso ndi madzi oyeretsera, ndipo chilichonse chimene chingathe kupsa ndi moto, muchiviike m'madzi omwewo. Muchape zovala zanu pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, ndipo mudzayeretsedwa. Pambuyo pake muloŵe ku mahema.” Chauta adauza Mose kuti, “Iwe, ndi wansembe Eleazara, pamodzi ndi atsogoleri a mabanja a mpingo, muŵerenge zofunkha zimene adalanda pa nkhondo, anthu pamodzi ndi nyama zomwe. Ndipo mugaŵe zofunkhazo magawo aŵiri, lina la ankhondo amene adaapita ku nkhondo, lina la mpingo wonse. Pa gawo la ankhondowo, mutengeko gawo la Chauta, pa zofunkha mazana asanu aliwonse mutengeko chimodzi, pa akapolo, pa ng'ombe, pa abulu ndi pa nkhosa. Mutenge zimenezo pa gawo la ankhondowo ndipo mupatse wansembe Eleazara, kuti zikhale zopereka zanu kwa Chauta. Ndipo pa gawo la Aisraele, mtengeko chofunkha chimodzi pa zofunkha makumi asanu aliwonse, pa anthu, ng'ombe, abulu, nkhosa ndi pa nyama zonse zoŵeta, ndipo mupatse Alevi amene amayang'anira Chihema cha Chauta.” Tsono Mose ndi wansembe Eleazara adachitadi zomwe Chauta adalamula Mose. Zofunkha zotsala zimene ankhondowo adalanda zinali izi: nkhosa 675,000, ng'ombe 72,000, abulu 61,000, ndi atsikana amene sadagonepo ndi amuna 32,000 pamodzi. Gawo la ankhondo amene adapita ku nkhondo linali nkhosa 337,500, ndipo gawo la Chauta linali nkhosa 675. Ng'ombe zinalipo 36,000, ndipo 72 zinali gawo la Chauta. Abulu analipo 30,500, ndipo 61 anali gawo la Chauta. Anthu analipo 16,000, ndipo 32 anali gawo la Chauta. Mose adapereka kwa wansembe Eleazara gawo limene linali loyenera kulipereka kwa Chauta, monga momwe Chauta adaalamulira Moseyo. Mose adagaŵa zofunkha napatsa Aisraele theka limodzi, kuchotsa pa zofunkha zonse zobwera ndi ankhondo aja. Tsono gawo la Aisraele linali ili: nkhosa 337,500, ng'ombe 36,000, abulu 30,500, ndiponso anthu 16,000. Pa gawo la Aisraelelo, Mose adatengako chofunkha chimodzi pa zofunkha makumi asanu aliwonse, anthu ndi nyama, ndipo adapatsa Alevi amene ankayang'anira Chihema cha Chauta, monga momwe Chauta adaalamulira Mose. Pamenepo akulu a nkhondo amene ankayang'anira ankhondo onse, ndiye kuti atsogoleri olamulira ankhondo zikwi, ndi atsogoleri olamulira ankhondo mazana, adabwera kwa Mose. Adauza Moseyo kuti, “Atumiki anufe taŵerenga ankhondo amene tikuŵalamulira, ndipo palibe munthu ndi mmodzi yemwe amene akusoŵa. Ndipo ife tabwera ndi zopereka kwa Chauta zimene munthu aliyense adapeza, monga golide, zibangiri, zikono, mphete zosindikizira, ndolo ndi mikanda, kuti achitire mwambo wopepesera machimo athu pamaso pa Chauta.” Apo Mose ndi wansembe Eleazara adalandira golide kwa atsogoleriwo, pamodzi ndi zinthu zonse zosula. Golide yense amene iwo adapereka kwa Chauta kuchokera kwa atsogoleri a ankhondo zikwi, ndi kwa atsogoleri a ankhondo mazana, anali wolemera makilogaramu 200 yense pamodzi. (Ankhondo aja anali atatenga zofunkha, aliyense zakezake.) Tsono Mose ndi wansembe Eleazara adalandira golideyo kwa atsogoleri a ankhondo zikwi ndi a ankhondo mazana, namuika m'chihema chamsonkhano, kuti akhale chikumbutso cha Aisraele pamaso pa Chauta. Ana a Rubeni ndi ana a Gadi anali ndi ng'ombe zambiri. Adaona dziko la Yazere ndi dziko la Giliyadi kuti linali ndi malo oyenera kuŵeterako ng'ombe. Choncho ana a Gadi ndi ana a Rubeni aja adabwera kwa Mose, kwa wansembe Eleazara ndi kwa atsogoleri a mpingo, naŵauza kuti, “Midzi ya Ataroti, Diboni, Yazere, Nimira, Hesiboni, Eleyale, Sibima, Nebo ndi Beoni, dziko limene Chauta adagonjetsera Aisraele, ndi dziko loyenera kuŵeterako ng'ombe, ndipo atumiki anufe tili ndi ng'ombe. Ngati mwatikomera mtima, mutipatse dzikoli atumiki anufe, kuti likhale lathu. Musatipititse patsidya pa Yordani.” Koma Mose adafunsa ana a Gadi ndi ana a Rubeni kuti, “Kodi abale anu azikamenya nkhondo, inu mutangokhala kuno? Chifukwa chiyani mufuna kuŵatayitsa mtima Aisraele, kuti asakaloŵe m'dziko limene Chauta adaŵapatsa? Makolo anu adachita zotero, pamene ndidaŵatuma kuchokera ku Kadesi-Baranea, kuti akaone dziko. Iwo atapita ku chigwa cha Esikolo, nakaona dzikolo, adatayitsa mtima Aisraele, pakuŵauza kuti asakaloŵe m'dziko limene Chauta adaŵapatsa. Tsono pa tsiku limenelo Chauta adapsa mtima, ndipo adalumbira kuti, ‘Ndithudi palibe ndi mmodzi yemwe mwa anthu otuluka m'dziko la Ejipito, kuyambira wa zaka makumi aŵiri ndi wopitirirapo, amene adzaone dziko limene ndidalonjeza kuti ndidzapatsa Abrahamu, Isaki ndi Yakobe, chifukwa sadanditsate kwathunthu. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaone dzikolo, kupatula Kalebe yekha mwana wa Yefune, Mkenizi uja, ndi Yoswa mwana wa Nuni, chifukwa iwoŵa ndiwo adatsata Chauta kwathunthu.’ Chauta adaŵapsera mtima Aisraele, ndipo adaŵayendetsa m'chipululu muja zaka makumi anai, mpaka udatha mbadwo wonse umene udachimwira Chauta. Tsopano inu mwaloŵa m'malo mwa makolo anu, inu mbadwo watsopano wa anthu ochimwa, ndipo mukufuna kuti muwonjezere mkwiyo woopsa wa Chauta pa Aisraele. Pakuti ngati muleka kumtsata, Iye adzasiyanso anthu m'chipululu, ndipo inu mudzaonongetsa anthu onseŵa.” Tsono iwo adasendera kwa Mose namuuza kuti, “Poyamba mutilole kuti timange kuno makola a nkhosa zathu, ndi mizinda yoti ana athu azikhalamo. Pambuyo pake tidzatenga zida zankhondo ndi kutsogolera Aisraele mpaka titakaŵafikitsa ku malo ao. Koma ana athu adzakhala m'mizinda yamalinga, chifukwa choopa anthu a m'dziko muno. Sitidzabwerera kwathu mpaka Mwisraele aliyense atalandira choloŵa chake. Ife ndiye sitidzalandira nao choloŵa chathu patsidya pa Yordanipo kapena patsogolo pake, chifukwa choti talandira choloŵa chathu tsidya lino la Yordani, kuvuma kuno.” Choncho Mose adauza anthuwo kuti, “Muchite izi: mutenge zida pamaso pa Chauta ndi kupita ku nkhondo. Aliyense mwa inu atenge zida, ndipo aoloke mtsinje wa Yordani pamaso pa Chauta ndi kupirikitsa adani ake patsogolo pake, mpaka kugonjetsa dzikolo pamaso pa Chauta. Mukatero, pambuyo pake mudzabwerera kuno, chifukwa mudzakhala mutagwirira ntchito Chauta ndi Aisraele. Pamenepo dziko lino lidzakhala lanu pamaso pa Chauta. Koma ngati simuchita choncho, mwachimwira Chauta, ndipo dziŵani kuti tchimo lanu lidzakutsatani. Mangani mizinda ya ana anu, ndi makola a nkhosa zanu, koma muchitedi zimene mwalonjeza.” Tsono ana a Gadi ndi ana a Rubeni adayankha Mose kuti, “Atumiki anu adzachitadi monga momwe inu mbuyathu mwalamulira. Ana athu ndi akazi athu atsala ku mizinda ya Giliyadi, pamodzi ndi nkhosa zathu ndi ng'ombe zathu zomwe. Koma atumiki anufe, tiwoloka aliyense atatenga zida, kukamenya nkhondo pamaso pa Chauta, monga momwe inu mbuyathu mwalamulira.” Choncho Mose adalamula wansembe Eleazara, Yoswa mwana wa Nuni, ndi atsogoleri a mabanja a mafuko a Aisraele kuti, “Ngati ana a Gadi ndi a Rubeni onse amene angathe kutenga zida kuti akamenye nkhondo pamaso pa Chauta. Adzaoloka nanu mtsinje wa Yordani, nadzagonjetsa dziko lili patsogolo panulo, mudzaŵapatse dziko la Giliyadi kuti likhale lao. Koma akapanda kuwoloka nanu, atatenga zida zankhondo, adzalandira chuma chao pakati panu m'dziko la Kanani.” Ndipo zidzukulu za Gadi ndi za Rubeni zidayankha kuti, “Ife atumiki anu tidzachita zomwe Chauta watiwuza. Tidzaoloka titatenga zida zankhondo pamaso pa Chauta, ndi kuloŵa m'dziko la Kanani, koma chuma cha choloŵa chathu chidzatsala ndi ife konkuno ku tsidya lino la Yordani.” Pomwepo Mose adapatsa ana a Gadi ndi a Rubeni ndiponso theka la fuko la Manase, mwana wa Yosefe, dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani, dziko lonse pamodzi ndi mizinda ndi milaga yake, ndiye kuti mizinda yonse ya m'dziko lonselo. Ana a Gadi adamanga mizinda ya Diboni, Ataroti, Aroere, Atiroti-Sofani, Yazere, Yogobeha, Betenimira ndi Beteharani. Yonseyo inali yozingidwa ndi malinga. Ndipo adamanganso makola a nkhosa. Ana a Rubeni adamanga mizinda ya Hesiboni. Eleyale, Kiriyataimu, Nebo, Baala-Meoni (dzina ili lidasinthidwa) ndi Sibima. Mizinda imene adamangayo adaitcha maina ena. A fuko la Makiri, mwana wa Manase, adapita kukalanda dziko la Giliyadi napirikitsa Aamori amene ankakhala m'dzikomo. Mose adapatsa Makiri mwana wa Manase dziko la Giliyadi, ndipo Makiriyo adakhala m'dziko limenelo. Yairi wa fuko la Manase adapita kukalanda midzi ina naitcha Havoti-Yairi. Noba adapita kukalanda mzinda wa Kenati pamodzi ndi midzi yake, ndipo adautcha Noba, kutengera dzina lake. Pamene Aisraele adatuluka m'dziko la Ejipito m'magulu a mafuko ao, Mose ndi Aroni akuŵatsogolera, Mose adalemba maina a malo onse oyambira ulendo ndi chigono chilichonse, monga Chauta adamlamula. Zigono zake potsata malo oyambira ulendo wao zinali motere: Adanyamuka ku Ramsesi pa mwezi woyamba, pa tsiku la 15 la mweziwo. M'maŵa mwake, litapita tsiku la Paska, Aisraele adatuluka m'dziko la Ejipito mokondwa, anthu onse a ku Ejipito akupenya. M'menemo nkuti Aejipitowo akuika maliro a ana ao achisamba amene Chauta adaaŵapha pakati pao. Choncho Chauta adalipsira milungu ya Aejipito. Pambuyo pake Aisraele adanyamuka ku Ramsesi nakamanga mahema ku Sukoti. Adanyamuka ku Sukoti nakamanga mahema ku Etamu, mzinda umene uli m'mbali mwa chipululu. Adanyamuka ku Etamu, nabwerera ku Pihahiroti, mzinda umene uli kuvuma kwa Baala-Zefoni. Ndipo adamanga mahema patsogolo pa Migidoli. Adanyamuka ku Pihahiroti naoloka pakatimpakati pa nyanja, ndipo adaloŵa m'chipululu. Tsono adayenda ulendo wa masiku atatu m'chipululu cha Etamu, nakamanga mahema ku Mara. Adanyamuka ku Mara nakafika ku Elimu. Ku Elimuko kunali akasupe khumi ndi aŵiri ndi mitengo ya migwalangwa makumi asanu ndi aŵiri, ndipo adamanga mahema ao kumeneko. Adanyamuka ku Elimu, nakamanga mahema ao m'mbali mwa Nyanja Yofiira. Adanyamuka ku Nyanja Yofiira, nakamanga mahema ao ku chipululu cha Sini. Adanyamuka ku chipululu cha Sini, nakamanga mahema ao ku Dofika. Adanyamuka ku Dofika, nakamanga mahema ao ku Alusi. Adanyamuka ku Alusi, nakamanga mahema ao ku Refidimu kumene kunalibe madzi akumwa. Adanyamuka ku Refidimu, nakamanga mahema ao ku chipululu cha Sinai. Adanyamuka ku chipululu cha Sinai, nakamanga mahema ao ku Kibroti-Hatava. Adanyamuka ku Kibroti-Hatava, nakamanga mahema ao ku Haseroti. Adanyamuka ku Hazeroti, nakamanga mahema ao ku Ritima. Adanyamuka ku Ritima, nakamanga mahema ao ku Rimoni-Perezi. Adanyamuka ku Rimoni-Perezi, nakamanga mahema ao ku Libina. Adanyamuka ku Libina, nakamanga mahema ao ku Risa. Adanyamuka ku Risa, nakamanga mahema ao ku Kehelata. Adanyamuka ku Kehelata, nakamanga mahema ao ku phiri la Sefera. Adanyamuka ku phiri la Sefera, nakamanga mahema ao ku Harada. Adanyamuka ku Harada, nakamanga mahema ao ku Makeloti. Adanyamuka ku Makeloti, nakamanga mahema ao ku Tahati. Adanyamuka ku Tahati, nakamanga mahema ao ku Tera. Adanyamuka ku Tera, nakamanga mahema ao ku Mitika. Adanyamuka ku Mitika, nakamanga mahema ao ku Hasimona. Adanyamuka ku Hasimona, nakamanga mahema ao ku Meseroti. Adanyamuka ku Meseroti, nakamanga mahema ao ku Beneyakana. Adanyamuka ku Beneyakana, nakamanga mahema ao ku Horo-Hagidigadi. Adanyamuka ku Horo-Hagidigadi, nakamanga mahema ao ku Yotibata. Adanyamuka ku Yotibata, nakamanga mahema ao ku Aborona. Adanyamuka ku Aborona, nakamanga mahema ao ku Eziyoni-Gebere. Adanyamuka ku Eziyoni-Gebere, nakamanga mahema ao m'chipululu cha Zini (ndiye kuti Kadesi). Adanyamuka ku Kadesi, nakamanga mahema ao ku phiri la Hori m'mbali mwa dziko la Edomu. Chauta atamlamula, wansembe Aroni adakwera phiri la Hori nakafera komweko, chaka cha 40 Aisraele atatuluka m'dziko la Ejipito, pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu. Aroniyo anali wa zaka 123 za kubadwa, pamene adamwalira pa phiri la Hori. Mfumu ya ku Aradi, Mkanani amene ankakhala m'dziko la Kanani, adamva kuti Aisraele akubwera. Pambuyo pake iwo adanyamuka ku phiri la Hori, nakamanga mahema ao ku Zalimona. Adanyamuka ku Zalimona, nakamanga mahema ao ku Punoni. Adanyamuka ku Punoni, nakamanga mahema ao ku Oboti. Adanyamuka ku Oboti, nakamanga mahema ao ku Iyeabarimu, m'dziko la Mowabu. Adanyamuka ku Iyimu, nakamanga mahema ao ku Dibonigadi. Adanyamuka ku Dibonigadi, nakamanga mahema ao ku Alimoni-dibulataimu. Adanyamuka ku Alimoni-dibulataimu, nakamanga mahema ao ku mapiri a Abarimu patsogolo pa Nebo. Adanyamuka ku mapiri a Abarimu, nakamanga mahema ao ku zigwa za ku Mowabu, pafupi ndi mtsinje wa Yordani ku Yeriko. Adamanga mahema ao pafupi ndi mtsinje wa Yordani kuyambira ku Beteyesimoti mpaka ku Abele-Sitimu, m'zigwa za Mowabu. Chauta adauza Mose m'zigwa za Mowabu pafupi ndi mtsinje wa Yordani, kuti, “Uza Aisraele kuti, Pamene muwoloka mtsinje wa Yordani kuti muloŵe m'dziko la Kanani, mudzapirikitse nzika zonse za m'dzikomo pamene mukufika, ndipo mudzaononge miyala yao yozokota ndi kuwononganso mafano ao osungunula. Mudzasakaze akachisi ao onse ku mapiri. Mudzalande dzikolo kuti likhale lanu, ndipo mudzakhale m'menemo, poti ndakupatsani kuti likhale lanu. Mudzalandira dzikolo kuti likhale choloŵa chanu mwamaere, potsata mabanja anu. Fuko lalikulu lilandire choloŵa chachikulu, ndipo fuko laling'ono lilandire choloŵa chaching'ono. Dziko lililonse limene maere agwere munthu, likhale lake la munthuyo. Mudzalandire choloŵa chanu potsata mafuko a makolo anu. Koma mukapanda kupirikitsa nzika zam'dzikomo pamene mukufika, amene mwaŵalola kuti atsalirewo adzakhala ngati zisonga zokubayani m'maso, ndiponso ngati minga m'mbali mwanu, ndipo adzakuvutani m'dziko m'mene mukakhalemo. Tsono ndidzakuchitani inuyo zimene ndinkaganiza kuti ndiŵachite iwowo.” Chauta adauza Mose kuti, “Ulamule Aisraele, uŵauze kuti, ‘Posachedwa muloŵa m'dziko la Kanani, (dziko limenelo ndilo lidzakhala choloŵa chanu, dziko lonse la Kananilo). Chigawo chakumwera cha dziko lanu chidzayambira ku chipululu cha Zini kulambalala malire a Edomu. Malire anu akumwera ayambira kuvuma, kumathero a Nyanja ya Mchere. Malire anuwo apite kumwera, ndipo akwere phiri la Akarabimu ndi kuwolokera ku Zini. Mathero ake akhale kumwera kwa Kadesi-Baranea. Tsono apitirire mpaka ku Hazaradara, ndipo alambalale kukafika ku Azimoni. Malirewo akhotere ku Azimoni ndi kumapita ku mtsinje wa ku Ejipito, ndipo akathere ku Nyanja.’ “Malire anu akuzambwe akhale Nyanja Yaikulu ndi gombe lake. Ameneŵa ndiwo malire akuzambwe. “Malire anu akumpoto ndi aŵa, mulembe malire kuyambira ku Nyanja yaikulu mpaka ku phiri la Hori. Kuchokera ku phiri la Horiko, mulembe malire kufikira ku chipata cha Hamati, ndipo mathero a malirewo akhale ku Zedadi. Tsono malirewo afike mpaka ku Zifuroni, ndipo mathero ake akhale ku Hazarenani. “Mulembe malire anu akuvuma kuyambira ku Hazarenaniko mpaka ku Sefamu. Atsike kuchokera ku Sefamu mpaka ku Ribula, kuvuma kwa Aini. Atsikebe mpaka ku gombe la Nyanja ya Galilea, kuvuma, atsike ndithu mpaka ku mtsinje wa Yordani, ndipo akathere ku Nyanja ya Mchere. Limeneli ndilo dziko lanu pamodzi ndi malire ake ozungulira dzikolo.” Mose adalamula Aisraele kuti, “limeneli ndilo dziko limene mudzalandira mwamaere kuti likhale choloŵa chanu, limene Chauta walamula kuti lipatsidwe kwa mafuko asanu ndi anai ndi theka. Fuko la ana a Rubeni mwa mabanja a makolo ao, ndi fuko la ana a Gadi mwa mabanja a makolo ao, pamodzi ndi theka la fuko la Manase, adalandira kale choloŵa chao. Mafuko aŵiriwo ndi thekalo adalandira kale choloŵa chao patsidya pa mtsinje wa Yordani ku Yeriko chakuvuma kotulukira dzuŵa.” Chauta adauza Mose kuti, “Maina a anthu amene adzakugaŵireni dzikolo kuti likhale choloŵa chanu, ndi wansembe Eleazara ndi Yoswa mwana wa Nuni. Mutenge mtsogoleri mmodzi pa fuko lililonse, kuti agaŵe dzikolo ngati choloŵa. Maina a anthuwo naŵa: M'fuko la Yuda akhale Kalebe mwana wa Yefune. M'fuko la ana a Simeoni akhale Semuele mwana wa Amihudi. M'fuko la Benjamini akhale Elidadi mwana wa Kisiloni. M'fuko la ana a Dani akhale Buki mwana wa Yogili. Mwa ana a Yosefe, m'fuko la ana a Manase akhale Haniyele mwana wa Efodi. M'fuko la ana a Efuremu akhale Kemuwele mwana wa Sifutani. M'fuko la ana a Zebuloni akhale Elizafani mwana wa Paranaki. M'fuko la ana a Isakara akhale Palatiele mwana wa Azani. M'fuko la ana a Asere akhale Ahihudi mwana wa Selomi. M'fuko la ana a Nafutali akhale Pedahele, mwana wa Amihudi. Ameneŵa ndiwo amene Chauta adalamula kuti agaŵe choloŵa cha Aisraele m'dziko la Kanani.” Chauta adauza Mose m'zigwa za Mowabu, pafupi ndi mtsinje wa Yordani, ku Yeriko, kuti, “Ulamule Aisraele kuti pa choloŵa chaocho, apatseko Alevi mizinda yoti azikhalamo. Ndipo Aleviwo muŵapatsenso mabusa pozungulira mizindayo. Mizindayo idzakhala yao yoti azikhalamo, ndipo mabusa ao adzakhala odyetseramo ng'ombe zao, zoŵeta zao ndi nyama zao zonse. Mabusa a mizindayo amene mudzapatse Aleviwo, adzayambire ku khoma la mzinda, adzatuluke kunja mamita 450, kuzungulira mzindawo. Uyese kunja kwa mzindawo, kuvuma mamita 900, kumwera mamita 900, kuzambwe mamita 900, kumpoto mamita 900, ndipo mzindawo ukhale pakati. Dziko limeneli lidzakhala busa la mizinda yaoyo.” “Mizinda imene mudzapatse Aleviyo idzakhale mizinda isanu ndi umodzi yothaŵirako, kumene muzidzalola kuti munthu wopha mnzake mwangozi athaŵireko. Ndipo mudzaŵapatsenso mizinda ina 42, kuwonjezera pa mizinda imeneyo. Mizinda imene mudzapatse Alevi idzakhale 48 yonse pamodzi, kuphatikizanso ndi mabusa ao. Pamene mukupatula mizinda imeneyi pa choloŵa cha Aisraele, muchotse mizinda yambiri pa mafuko aakulu, ndipo muchotse mizinda pang'ono pa mafuko aang'ono. Fuko lililonse lidzapereka kwa Alevi molingana ndi kukula kwa choloŵa chimene lalandira.” Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Uza Aisraele kuti: Pamene muwoloka mtsinje wa Yordani ndi kuloŵa m'dziko la Kanani, mupatule mizinda ina kuti ikhale mizinda yanu yothaŵirako, kumene munthu wopha mnzake mwangozi azithaŵirako. Mizindayo idzakhala malo obisalamo pothaŵa munthu wofuna kubwezera choipa, kuti munthu wopha mnzake mwangoziyo asaphedwe, mpaka akaime pamaso pa mpingo kuti umuweruze. Mizinda imene mudzaperekeyo idzakhala mizinda isanu ndi umodzi yothaŵirako. Mudzapereke mizinda itatu patsidya la kuvuma la mtsinje wa Yordani, ndi mizinda itatu m'dziko la Kanani, kuti ikhale mizinda yothaŵirako. Mizinda isanu ndi umodziyo idzakhala yothaŵirako Aisraele, alendo ndi anthu okhala pakati pao, kuti wina aliyense wopha munthu mnzake mwangozi azithaŵirako. “Koma ngati munthu amenya mnzake ndi chitsulo, mnzakeyo nkufa, ndiye kuti ndi wopha munthu ameneyo. Ndipo wopha mnzakeyo ayenera kuphedwa. Ngati munthu amenya mnzake ndi mwala, mwala wake woti nkupha munthu, mnzakeyo nafadi, ndiye kuti ndi wopha munthu ameneyo. Tsono wopha mnzakeyo ayenera kuphedwa. Kapena munthu akamenya mnzake ndi chibonga choti nkupha munthu, mnzakeyo nafadi, ndiye kuti ndi wopha munthu ameneyo. Tsono wopha mnzakeyo ayenera kuphedwa. Mbale wake wa munthu wakufayo ndiye adzaphe wopha mnzakeyo. Akadzangokumana, wopha mnzakeyo adzamuphe ndi munthu wolipsira magaziyo. Ndipo ngati munthu abaya mnzake chifukwa cha chidani, kapena amulasa ndi chida atamubisalira, mnzakeyo naafa, kapena kumpanda ndi dzanja lake modana naye, mnzakeyo naafa, ndiye kuti amene adamenya mnzakeyo ayenera kuphedwa. Ndi wopha munthu ameneyo. Mbale wa munthu wakufayo ndiye aphe wopha mnzakeyo akangokumana naye. “Koma ngati munthu abaya mnzake mwangozi osati chifukwa cha chidani, kapena alasa mnzake ndi chida osamubisalira, kapena amulasa ndi mwala woti nkupha munthu, koma amlasa osamuwona mnzakeyo, pamenepo mpingo uweruze pakati pa munthu wopha mnzakeyo ndi mbale wa munthu wakufayo, potsata malangizo ameneŵa. Mpingo umpulumutse munthu wopha mnzakeyo m'manja mwa mbale wa munthu wakufayo. Ndipo um'bweze munthuyo ku mzinda wake wothaŵirako kumene adathaŵira. Adzakhala komweko mpaka mkulu wa ansembe onse atamwalira. Koma ngati munthu wopha mnzake mwangoziyo atuluka nthaŵi iliyonse kunja kwa malire a mzinda umene adathaŵiramo, ndipo mbale wa munthu wakufa uja ampeza ali kunja kwa malire a mzindawo, nkupha wopha mnzake uja, sadzapalamula mlandu wopha munthu. Pajatu munthuyo ayenera kukhala mu mzinda umene adathaŵiramo mpaka mkulu wa ansembe onse atamwalira. Koma mkulu wa ansembe onse atamwalira, wopha mnzakeyo angathe kubwerera ku dziko lake. “Zimenezi zikhale malamulo ndi malangizo kwa inu pa mibadwo yanu yonse kulikonse kumene mukakhale. Ngati wina aliyense apha mnzake, wopha mnzakeyo ayenera kuphedwa, mboni zitapereka umboni wao. Koma munthu asaphedwe pamene munthu mmodzi yekha wapereka umboni. Kuwonjezera apo, musalandire dipo loombolera munthu wopha mnzake amene wapalamula mlandu wopha munthu. Koma munthu ameneyo ayenera kuphedwa ndithu. Ndipo musalandire dipo loombolera munthu amene ali mu mzinda wake wothaŵirako kuti abwerere ndi kukakhala ku dziko lake, mkulu wa ansembeyo asanamwalire. Musaipitse dziko limene mukukhalamolo. Magazi amaipitsa dziko, ndipo nkosatheka kulipirira dziko chifukwa cha magazi amene akhetsedwa m'menemo, kupatula pokhetsa magazi a munthu amene adakhetsa magaziyo. Musaipitse dziko limene mukukhalamo, dziko limene Inenso ndikukhalamo. Paja Ine Chauta ndimakhala pakati pa Aisraele.” Atsogoleri a banja la ana a Giliyadi mwana wa Makiri, mwana wa Manase, limodzi mwa mabanja a adzukulu a Yosefe, adabwera kudzalankhula ndi Mose ndi atsogoleri, akulu a mabanja a makolo a Aisraele. Iwowo adati, “Chauta adakulamulani inu mbuyathu kuti mutachita maere, mupatse Aisraele dziko, kuti likhale choloŵa chao. Ndiponso inu mbuyathu, Chauta adakulamulani kuti mupatse choloŵa cha mbale wathu Zelofehadi kwa ana ake aakazi. Koma ngati akwatiwa ndi amuna a mafuko ena a Aisraele, choloŵa chao chidzachotsedwa pa choloŵa cha makolo athu ndi kuwonjezera pa choloŵa cha fuko la amuna aowo, motero choloŵa chathu chidzachepa. Ndipo chikafika chikondwerero cha Aisraele cha chaka cha 50, choloŵa chaocho chidzaonjezedwa pa choloŵa cha fuko la amuna ao. Motero choloŵa chao chidzachotsedwa pa choloŵa cha fuko la makolo athu.” Pamenepo Mose adaŵalamula Aisraele potsata mau a Chauta, adati, “Zimene akunena ana a Yosefezi nzoona. Zomwe Chauta akulamula za ana aakazi a Zelofehadi ndi izi: Aloleni akwatiwe ndi yemwe akumufuna, malinga akwatiwe ndi a m'banja la fuko la makolo ao. Choloŵa cha Aisraele chisachotsedwe m'fuko lina nkuchipatsa fuko lina. Pakuti Mwisraele aliyense ayenera kukangamira pa choloŵa cha fuko la makolo ake. Mkazi aliyense amene alandira choloŵa m'fuko lililonse la Aisraele, akwatiwe ndi ana a abale a bambo wao. Mwisraele aliyense adzalandira choloŵa cha makolo ake. Choncho palibe choloŵa chimene chidzachotsedwe m'fuko lina kupatsidwa ku fuko lina. Pajatu fuko lililonse la Aisraele lidzakangamira pa choloŵa chake.” Ana aakazi a Zelofehadi adachitadi zomwe Mulungu adalamula Mose. Mala, Tiriza, Hogola, Milika ndi Nowa, ana aakazi a Zelofehadi, adakwatiwa ndi ana a abale a bambo wao. Adakwatiwa ndi a m'mabanja a ana a Manase mwana wa Yosefe, ndipo choloŵa chao chidakhalabe m'fuko la bambo wao. Ameneŵa ndiwo malamulo ndi malangizo amene Chauta adalamula Aisraele kudzera mwa Mose. Adaperekedwa m'zigwa za Mowabu, pafupi ndi mtsinje wa Yordani ku Yeriko. Naŵa mau amene Mose adauza Aisraele onse pamene anali m'chipululu, patsidya pa mtsinje wa Yordani, m'chigwa cha Araba, kuyang'anana ndi Sufu, pakati pa Parani tsidya lina ndi Tofele, Labani, Hazeroti ndi Dizahabu tsidya linanso. Ulendo wa pakati pa Horebu ndi Kadesi-Baranea, kudzera njira ya phiri la Seiri, unali wa masiku 11. Pa tsiku loyamba la mwezi wa 11, pa chaka cha 40 kuyambira pamene adatuluka m'dziko la Ejipito, Mose adauza anthu a ku Israele zonse zimene Chauta adamlamula kuti anene kwa anthuwo. Zimenezi zidachitika Moseyo atagonjetsa kale Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankakhala ku Hesiboni, ndi mfumu Ogi wa ku Basani, amene ankakhala ku Asitaroti ndi ku Ederei. Mose adayamba kufotokozera anthu malamuloŵa ku tsidya la Yordani m'dziko la Mowabu, adati: Pamene tinali ku phiri la Horebu, Chauta, Mulungu wathu, adatiwuza kuti, “Inu mwakhalitsa kuphiri kuno. Nyamukani muyambepo kuyenda. Pitani ku dziko lamapiri la Aamori, ndi konse kumene kumakhala anzao a Aamoriwo ku chigwa cha Araba, ku dziko lamapiri ndi ku zigwa, ku Negebu ndi pamphepete pa Nyanja yaikulu, ku dziko la Akanani ndi ku Lebanoni, mpaka ku mtsinje waukulu wa Yufurate. Ndi limenelitu dziko limene ndikulipereka kwa inu. Muloŵe ndi kukhazikika m'dzikoli limene Ine Chauta, Mulungu wanu, ndidalumbira kuti ndidzapatsa makolo anu, Abrahamu, Isaki ndi Yakobe, ndi zidzukulu zao zonse.” Mose adatinso: Paja ndidakuuzani nthaŵi imeneyo kuti sindingathe kusenza ndekha udindo wokutsogolerani. Chauta, Mulungu wanu, wakuchulukitsani mpaka lero muli ngati nyenyezi zamumlengalenga. Chauta, Mulungu wa makolo anu, akulitse chiŵerengero chanu pochichulukitsa ndi chikwi chimodzi, ndipo akudalitseni monga momwe adalonjezera. Koma ine ndekha ndingathe bwanji kusenza udindo wokutsogolerani ndi womaweruzanso milandu pakati panu? Sankhani anthu ena anzeru, omvetsa ndi odziŵa zinthu bwino, pakati pa mafuko anu, ndipo ine ndidzaŵaika kuti akhale atsogoleri pakati panu. Ndipo inu mudaandiyankha kuti, “Zimene mwanenazi nzabwino, ife tidzachitadi.” Motero ndidasankha atsogoleri anu, anthu anzeru ndi odziŵa zinthu bwino, ndipo ndidaŵaika kuti aziyang'anira ena magulu a anthu zikwi zingapo, ena a anthu mazana angapo, ena a anthu makumi asanu, ndipo enanso a anthu khumi. Enanso ndidaŵasankha kuti akhale nduna pakati pa mafuko anuwo. Pa nthaŵi imene ija, ndidaŵalangiza aweruzi anuwo kuti, “Mumve milandu imene ili pakati pa anthu anu. Mlandu uliwonse muuweruze bwino, kaya ndi wa anthu a mtundu wanu, kapena wa alendo amene amakhala nao pakati panu. Musamakondere poweruza. Aliyense, munthu wamba kapena wamkulu, mumuweruze chimodzimodzi. Musamaopa wina aliyense, chifukwa chiweruzo chonse ndi cha Mulungu. Mlandu wina ukakulakani, mubwere nawo kwa ine, ndipo ndidzaugamula ndine.” Nthaŵi yomweyo, ndidakuuzani zonse zimene muyenera kuchita. Ife tidachita zimene Chauta, Mulungu wathu, adatilamula. Tidachoka ku phiri la Horebu ndipo tidabzola chipululu chachikulu ndi choopsa chija chimene mudachiwona pa njira yopita ku dziko lamapiri la Aamori. Titafika ku Kadesi-Baranea, ndidakuuzani kuti, “Tsopano, tafika ku dziko lamapiri la Aamori limene Mulungu wa makolo athu akutipatsa. Ndi limenelitu dziko lomwe Chauta, Mulungu wa makolo anu, akukupatsani. Pitani, kakhaleni m'menemo monga momwe adakulamulirani. Musaope kapena kuchita mantha.” Koma paja inu mudabwera kwa ine nkumanena kuti, “Tiyeni titume anthu akaliwone dzikolo, kuti adzatiwuze njira yabwino yoti tidzadzere, ndipo adzatifotokozere za m'mene iliri mizinda yakumeneko.” Mau amenewo adandikomera, motero ndidasankha anthu khumi ndi aŵiri, mmodzi pa fuko lililonse. Iwoŵa adanyamuka napita ku dziko lamapirilo, mpaka adakafika ku chigwa cha Esikolo, ndipo adakalizonda dzikolo. Adabwerera atatengako zipatso, nafika nazo pakati pathu. Ndipo adatiwuza kuti, “Dziko limene Chauta, Mulungu wathu, akutipatsalo ndi lachonde.” Koma inu simudafune kupita, mudaukira ulamuliro wa Chauta, Mulungu wanu. Inu munkangodandaula m'mahema mwanu nkumati, “Chauta amadana nafe. Nchifukwa chake adatitulutsa ku dziko la Ejipito, natipereka kwa Aamori kuti atiphe. Kodi tikapeza dziko lanji kumeneko? Abale athu aja atidederetsa potiwuza kuti anthu akumeneko ngamphamvu ndi aatali kupambana ife. Akutinso mizindayo njaikulu, ya malinga ofika mpaka m'mwamba. Ndiponso akuti kumeneko adaona ziphona, zidzukulu za Aanaki.” Koma ine ndidakuuzani kuti, “Musaŵaope anthu amenewo. Chauta, Mulungu wanu, ndiye amene adzakutsogolerani, ndipo adzaponyanso nkhondo m'malo mwanu, monga momwe mudaonera ku Ejipito kuja ndi m'chipululu muja. Inu mudaona njira yonse m'mene adakufikitsirani kuno, kuti adakunyamulani monga momwe bambo amanyamulira mwana wake.” Koma ngakhale zidachitika zimenezo, inu simudakhulupirire Chauta, Mulungu wanu, amene nthaŵi zonse ankatsogola pa ulendo wanu, kuti akupezerenitu malo omangapo mahema anu. Iye ankayenda patsogolo panu m'maonekedwe a moto usiku, kuti akuunikireni njira, koma masana ankakhala ndi maonekedwe a mtambo. Chauta atamva kudandaula kwanuko, adakwiya ndipo adalumbira kuti, “Mu mbadwo woipitsitsawu palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaloŵe m'dziko lachondelo limene ndidalumbira kuti ndidzapatsa makolo anu. Koma Kalebe yekha, mwana wa Yefune, ndiye amene adzaloŵe. Iyeyo adakhala ndithu wokhulupirika kwa Ine, choncho dziko adalipenyalo ndidzalipatsadi kwa iye ndi kwa zidzukulu zake.” Chauta adandikwiyira inenso chifukwa cha inu. Adati, “Iwe Mose sudzaloŵa m'dzikomo, koma mthandizi wako Yoswa, mwana wa Nuni, ndiye adzaloŵe. Umlimbitse mtima Yoswayo, poti iyeyo ndiye adzatsogolere Aisraele pokaloŵa m'dzikomo.” Tsono Chauta adatiwuza tonsefe kuti, “Makanda anu amene mudati adzagwidwa ndi adani, ndiponso ana anu amene akadali aang'ono, amene sadziŵa chabwino kapena choipa pa lero lino, ndiwo adzaloŵe m'dzikolo. Ndidzalipatsa kwa iwowo ndipo adzakhalamo. Koma inu bwererani, muzipita ku chipululu, kulunjika ku Nyanja Yofiira.” Inu mudayankha kuti, “Ife tachimwira Chauta. Koma tsopano tidzamenya nkhondo monga momwe Chauta wathu adatilamulira.” Pamenepo aliyense mwa inu adatenga zida zake zankhondo, namaganiza kuti nkwapafupi kugonjetsa dziko lamapirilo. Koma Chauta adandiwuza kuti, “Uŵachenjeze kuti asaŵapute Aamoriwo, chifukwa Ine sindidzakhala nawo, ndipo adani aowo adzaŵagonjetsa.” Ndidakuuzani zimene Chauta adanena, koma inu simudasamale. Mudaukira Chauta, ndipo mudakaloŵa m'dziko lamapirilo, muli tumbatumba kunyada. Pamenepo Aamori okhala m'mapiriwo adakutulukirani nakuthamangitsani ngati njuchi, ndipo adakukanthani kuchokera ku Seiri mpaka ku Horoma. Tsono inu pobwera mudalira kuti Chauta akuthandizeni, koma Chauta sadakumvereni kapena kukutcherani khutu. Nchifukwa chake mudakhalako masiku ambiri ku Kadesi. Tidabwerera kupita ku chipululu podzera njira ya ku Nyanja Yofiira, monga momwe Chauta adatilamulira. Ndipo tidakhala tikuzungulira phiri la Seiri masiku ambiri. Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Mwakhala mukuyenda uku ndi uku mozungulira dziko lamapirili nthaŵi yokwanira, tsopano tembenukani, mupite kumpoto. Mulangize anthu kuti: Muli pafupi kubzola dziko la achibale anu, zidzukulu za Esau, amene akukhala m'Seiri. Iwowo adzakuwopani inu, koma inu muchenjere, musaŵapute, popeza kuti sindidzakupatsani dziko laolo, ngakhale mpoti muponde pomwe. Phiri la Seiri ndalipereka kwa zidzukulu za Esau. Chakudya mudzachita chogula ndi ndalama, madzi akumwanso mudzachita ogula ndi ndalama.” Chauta, Mulungu wanu, wakudalitsani pa ntchito zonse zimene mwachita. Wakusamalirani pa ulendo wanu m'chipululu chachikuluchi. Chauta, Mulungu wanu, wakhala nanu pa zaka makumi anai zonsezi, ndipo simudasoŵe kanthu kalikonse. Tsono tidapitirira ulendo wathu molambalala dziko la Seiri kumene kunali zidzukulu za Esau, ndipo tidasiya njira ya Araba yochokera ku mizinda ya Elate ndi Eziyoni-Gebere. Choncho tidatembenuka ndi kulunjika ku chipululu cha Mowabu. Ndipo Chauta adandiwuza kuti, “Musaŵavute Amowabu, zidzukulu za Loti. Musachite nawo nkhondo. Iwoŵa ndaŵapatsa dziko la Ari, ndipo sindikupatsani ngakhale gawo lomwe la dziko laolo.” (Kale ku Ari kunkakhala mtundu wina wa anthu otchedwa Aemimu. Anthu ake anali otchuka ndiponso ambiri. Kutalika kwao ankalingana ndi mtundu wina wa anthu otchedwa Aanaki. Monga Aanaki omwe, anthuwo ankadziŵika ndi dzina lakuti Arefaimu. Koma Amowabu ankaŵatchula kuti Aemimu. Ahorinso ankakhala ku Seiri, koma zidzukulu za Esau zidaŵapirikitsa, ndi kuwononga mtundu wonse. Atatero, iwo adakhala ku dziko la Seiri. Adachita zimenezi monga momwe Aisraele adapirikitsira adani ao m'dziko limene Chauta adaŵapatsa.) Tsono Chauta adaonjeza kuti, “Tsopano nyamukani, muwoloke mtsinje wa Zeredi.” Choncho tidaoloka mtsinje wa Zeredi. Nthaŵi imene tidaoloka mtsinje wa Zerediwo, nkuti patapita kale zaka 38 kuyambira pamene tidakhala ku Kadesi-Baranea. Amuna odziŵa kumenya nkhondo nkuti atafa onse, monga momwe adaanenera Chauta molumbira. Zoonadi dzanja la Chauta lidaŵakantha mpaka onse am'mahemawo adatha nkuwonongeka. Amuna onse omenya nkhondo atafa, Chauta adandiwuza kuti, “Lero mudutsa dziko la Amowabu, podzera njira ya ku Ari. Tsono mukadzafika pafupi ndi dziko la Aamoni, musaŵavute kapena kuchita nawo nkhondo, chifukwa sindikupatsani dziko lao, popeza kuti dzikolo ndidalipereka kwa zidzukulu za Loti, kuti likhale laolao.” (Dziko limeneli linalinso dziko la Arefaimu, chifukwa kale iwowo ankakhala m'dziko limeneli. Aamoni ankaŵatchula kuti Azamzumimu. Kutalika kwao ankalingana ndi Aanaki. Anali anthu otchuka ndiponso ochuluka kwambiri. Komabe Chauta adaŵaononga, ndipo dziko lao lidatengedwa ndi Aamoni amene adakhazikika kumeneko. Zimenezi ndi zomwe Chauta adaachita ndi zidzukulu za Esau zimene zinkakhala ku Seiri. Iye adaononga Ahori, ndipo dziko lao lidatengedwa ndi ana a Esauwo, nakhazikika kumeneko, ndipo akukhalako mpaka lero lino. Kunena za Avimu amene ankakhala m'midzi yonse mpaka ku Gaza, dziko lao adalilanda ndi Akafitori ochokera ku Kafitori, amene adakhazikika kumeneko ataononga Avimu aja.) Tsono Chauta adaonjeza kuti, “Nyamukani tsopano, tiyeni, muwoloke mtsinje wa Arinoni. Ndikukupatsani Sihoni Mwamoriyo, mfumu ya Hesiboni, pamodzi ndi dziko lake lomwe. Mputeni, ndipo muyambepo kumenyana naye nkhondo. Ndiyamba lero kuŵachititsa mantha anthu a pa dziko lapansi kuti azikuwopani. Aliyense akangomva za inu, adzanjenjemera ndi mantha ndi kuda nkhaŵa chifukwa choopa inu.” Tsono ndidatuma amithenga kuchokera ku chipululu cha Kedemoti, kuti apite kwa mfumu Sihoni wa ku Hesiboni. Poŵatumapo, ndidaŵauza kuti akanene mau amtendere, kuti, “Tiloleni, tidzere m'dziko mwanu. Tidzangodutsa dziko lanulo molunjika podzera mu mseu osapatuka uku ndi uku. Chakudya mudzachita chotigulitsa, madzi akumwanso mudzachita otigulitsa. Mungotilola kuti tidzere m'dziko mwanu, kuti tiwoloke mtsinje wa Yordani ndi kukafika ku dziko limene Chauta, Mulungu wathu, akutipatsa. Zidzukulu za Esau ku Edomu, ndi Amowabu ku Ari, onsewo adatilola kudzera m'maiko mwao.” Koma mfumu Sihoni yekha sadatilole kuti tidzere m'dziko mwake. Chauta, Mulungu wanu, adamuumitsa khosi nampatsa mtima wouma, kuti ampereke m'manja mwathu monga momwe mukuwonera lero lino. Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Taona ndayamba kale kukupatsa mfumu Sihoni ndi dziko lake lomwe. Uyambe kulilandadi, kuti mukakhale ndithu m'menemo.” Pamenepo Sihoni pamodzi ndi anthu ake adabwera kudzalimbana nafe pafupi ndi mudzi wa Yahazi. Koma Chauta, Mulungu wathu, adampereka kwa ife, ndipo tidamgonjetsa iyeyo pamodzi ndi ana ake ndi anthu ake omwe. Tidalandanso ndi kuwonongeratu midzi yake yonse, ndi kupha amuna ndi akazi onse ndi ana omwe. Sitidasiyepo wamoyo ndi mmodzi yemwe. Ng'ombe zokha tidasunga ngati zofunkha zathu, pamodzi ndi chuma cha m'mizinda imene tidalandayo. Kuchokera ku Aroere, mzinda umene uli pamphepete pa mtsinje wa Arinoni, ndiponso kuchokera ku mzinda umene uli m'dambomo mpaka ku Giliyadi, panalibe mzinda wa malinga aatali ndi umodzi womwe umene udatikanika kugwetsa. Chauta adatithandiza kulanda mizinda yonse. Koma ku dziko la Aamoni sitidadzereko, ndiye kuti m'mbali mwa mtsinje wa Yaboki kapena kuti mizinda ya ku dziko lamapiri, kapenanso kwina kulikonse kumene Chauta, Mulungu wathu, adaatiletsa kupitako. Pambuyo pake tidapitirira ulendo kulunjika ku Basani. Mfumu Ogi pamodzi ndi anthu ake onse, adatuluka kudzatithira nkhondo pafupi ndi mudzi wa Ederei. Koma Chauta adandiwuza kuti, “Usamuwope, poti iyeyo, anthu ake, pamodzi ndi dziko lake lomwe, ndakupatsa iwe. Umchite zomwe udachita Sihoni, mfumu ya Aamori, amene ankalamulira ku Hesiboni.” Motero Chauta adapereka mfumu Ogi ndi anthu ake m'manja mwathu, ndipo tidaŵapha onsewo osatsalapo ndi mmodzi yemwe. Tidalandanso mizinda yake yonse nthaŵi yomweyo, sitidasiyeko ndi umodzi womwe. Mizinda yonse imene tidalanda inali makumi asanu ndi limodzi, dera lonse la Arigobu, kumene mfumu Ogi wa ku Basani ankalamulira. Mizinda yonseyi inali yotchinjirizidwa ndi malinga ataliatali, ndiponso ya zipata zokhala ndi mipiringidzo yake. Panalinso midzi yambirimbiri yopanda malinga. Tidaononga midziyo ndi mizinda yonse, ndipo tidapha onse amuna ndi akazi ndi ana omwe, monga momwe tidachitira mizinda ya mfumu Sihoni wa ku Hesiboni. Kenaka tidafunkha zoŵeta ndi chuma cha m'mizinda yonseyo. Tsono pa nthaŵi imeneyo mafumu aŵiri a Aamoriwo tidaŵalanda dziko patsidya pa Yordani, kuchokera ku chigwa cha mtsinje wa Arinoni mpaka ku phiri la Heremoni. (Asidoni potchula phiri la Heremoni ankati Sirioni, koma Aamori potchula phiri lomwelo ankati Seniri.) Tidalandanso mizinda yakumapiri, dziko lonse la Giliyadi ndi Basani, mpaka ku Saleka ndi Ederei, mizinda ya ufumu wa Ogi ku Basani. (Ogi yekha, mfumu ya ku Basani, ndiye amene adatsala mwa Arefaimu. Kama lake linali lachitsulo, m'litali mwake linali la mamita anai, muufupi mwake mamita aŵiri, polinganiza ndi miyeso ya nthaŵi imeneyo. Kamalo angathe kuchiwonabe ku Raba, mzinda wa Aamoni.) Dzikolo titalanda, ndidagaŵira fuko la Rubeni ndi la Gadi dera lija kuyambira ku Aroere, pafupi ndi mtsinje wa Arinoni, ndiponso theka la dziko lamapiri la Giliyadi, pamodzi ndi mizinda yake. Theka la fuko la Manase, ndidalipatsa dera lonse la Giliyadi limene lidatsalira, ndiponso Basani dziko la mfumu Ogi uja, ndiye kuti dera lonse la Arigobu. (Basani linkadziŵika ndi dzina loti dziko la Arefaimu. Yairi, wa fuko la Manase, adatenga dera lonse la Arigobu, ndiye kuti Basani, mpaka kukafika ku malire a Gesuri ndi Maaka. Mizindayo adaitchula dzina lake, ndipo mpaka lero lino, imadziŵika kuti ndi ya Yairi.) Dziko la Giliyadi ndidalipereka kwa Makiri wa fuko la Manase. Dziko lonse kuchokera ku Giliyadi mpaka ku chigwa cha Arinoni, ndidapatsa fuko la Rubeni ndi la Gadi. Pakatimpakati pa chigwa cha Arinoni ndiye panali malire akumwera, ndipo malire ake akumpoto anali mtsinje wa Yaboki, umene mbali yake inali malire a dziko la Aamoni. Chakuzambwe dziko lao linkafika mpaka ku mtsinje wa Yordani, kuchokera ku Kinereti kumpoto, mpaka kukafika ku Nyanja ya Araba, ndiye kuti Nyanja yamchere kumwera. Ndipo chakuvuma linkafika pa tsinde la phiri la Pisiga. Pa nthaŵi imeneyo ndidaakulamulani kuti, “Chauta, Mulungu wathu, ndiye wakupatsani dzikoli kuti likhale lanu. Amuna onse otha kumenya nkhondo atenge zida ndipo atsogolere abale anu, mafuko a Aisraele. Koma akazi anu okha ndi ana anu adzakhalira m'mizinda imene ndidakupatsani, pamodzi ndi ng'ombe zanu zomwe. (Ndikudziŵa kuti muli ndi ng'ombe zambiri.) Muŵathandize Aisraele anzanu mpaka akhazikike mwamtendere m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu waŵapatsa kuzambwe kwa Yordani, monga momwe Chauta adakuchitirani inu. Pambuyo pake aliyense mwa inu adzabwere ku dera limene ndidakupatsani.” Pamenepo ndidauza Yoswa kuti, “Wapenya zonse zimene Chauta, Mulungu wanu, adaŵachita mafumu aŵiri aja Sihoni ndi Ogi. Tsono ena onse amene muŵathire nkhondo m'maiko ao, adzaŵachita chimodzimodzi. Musaŵaope, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, ndiye amene adzaponye nkhondo pamodzi nanu.” Pa nthaŵi imeneyo, ndidapemphera kwa Chauta kuti, “Inu Ambuye Chauta, mwangondiwonetsa chiyambi chake chokha cha ntchito za ukulu wanu ndi mphamvu zanu. Kumwambako, ngakhalenso pansi pano, palibe Mulungu wina amene angathe kuchita zinthu zamphamvu zonga zimene inu mumachita. Inu Chauta, mundilole kuti ndingooloka mtsinje wa Yordani wokhawu, ndipo kuti ndiwone dziko labwinolo patsidyapo, dziko lokongola lamapiri, ndiponso mapiri a Lebanoni.” Koma Chauta anali wondikwiyira ine chifukwa cha inu, ndipo sadandimvere konse. M'malo mwake adangoti, “Pakwana! Usanenenso zimenezi! Kwera pa nsonga ya phiri la Pisiga, ndipo uyang'ane kumpoto ndi kumwera, kuvuma ndi kuzambwe. Uyang'anitsitse bwino zimene uziwonezo, chifukwa iwe suwoloka Yordani. Koma umlangize bwino Yoswayu ndi kumlimbitsa mtima, chifukwa iyeyu ndiye atsogolere anthuŵa kuwoloka mpaka tsidya linalo, ndi kukakhala m'dziko limene udzaliwonalo.” Motero tidatsalira ku chigwa, moyang'anana ndi mzinda wa Betepeori. Tsopano inu Aisraele, muzimvera malamulo ndi malangizo onse amene ndikukuphunzitsani, kuti mukhale ndi moyo. Ndipo mudzaloŵa ndi kukhazikika m'dziko limene Chauta, Mulungu wa makolo anu, akukupatsani. Musaonjezerepo kanthu kena pa zimene ndakulamulani, ndipo musachotsepo kanthu. Muzimvera malamulo a Chauta, Mulungu wanu, amene ndakupatsani. Inu mudaona zimene Chauta adachita ku Baala-Peori. Kumeneko Chauta, Mulungu wanu, adaonongeratu onse amene ankapembedza Baala wa ku Peori, koma nonsenu amene mudakangamira Chauta, Mulungu wanu, muli ndi moyo lero lino. Ndakuphunzitsani malamulo ndi malangizo onse, monga momwe Chauta, Mulungu wanga, adandilamulira. M'dziko limene mudzaloŵa ndi kukhalamolo, muzikamvera malamulo ameneŵa. Mukaŵasunge ndi kuŵatsata, ndipo chimenechi chidzaonetsa anthu a mitundu ina kuti ndinu anthu anzeru ndi omvetsa zinthu bwino. Akadzamva malamulo onseŵa, iwowo adzati, “Mtundu umenewu ndi waukulu, wanzeru ndi womvetsa zinthu bwino.” Palibe mtundu wina uliwonse, kaya ndi waukulu chotani, umene uli ndi Mulungu wokhala pafupi nawo, monga m'mene Mulungu wathu amakhalira ndi ife. Nthaŵi zonse tikamuitana, amatiyankha. Palibe mtundu wina uliwonse kaya ndi waukulu chotani, umene uli ndi malamulo ndi malangizo achilungamo onga aŵa amene ndakupatsani leroŵa. Mukhale tcheru, ndipo musadzaiŵale zonse zimene mudaziwona. Zimenezo zisachoke m'mitima mwanu pa moyo wanu wonse. Muzizifotokoza kwa ana anu ndi kwa zidzukulu zanu zomwe. Muziŵauza za tsiku lija pamene mudaima pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, ku phiri la Horebu kuja. Kumeneko Chauta adandiwuza kuti, “Asonkhanitseni anthu. Ndifuna kuti iwo amve zimene ndilankhule, kuti aphunzire kundiwopa nthaŵi zonse adzakhale ndi moyo pa dziko lapansi, kenaka azidzaphunzitsanso ana ao kundimvera.” Inu mudadza, mudaima patsinde pa phiri. Phirilo linkayaka moto mokwera mpaka ku thambo, ndipo linali lophimbidwa ndi chiwutsi chabii ndi chimdima. Chauta adalankhula nanu ali m'motomo, ndipo munkamumva akulankhula, koma osamuwona. Chauta adakuuzani zimene muyenera kuchita, kuti musunge chipangano chimene adapangana ndi inu, ndicho malamulo khumi amene adaŵalemba pa miyala iŵiri. Chauta adandilamula nthaŵi imeneyo kuti ndikuphunzitseni malamulo amene muyenera kumaŵasunga m'dziko limene mukaloŵe ndi kukakhalamolo. Pamene Chauta adalankhula nanu ali m'moto pa phiri la Horebu lija, inu simudaone kanthu kalikonse. Nchifukwa chake muchenjere. Samalani kuti musachimwe pakudzipangira fano la mtundu uliwonse, kaya fanolo likhale longa mwamuna kaya mkazi, fano la nyama iliyonse ya pa dziko lapansi, fano la mbalame iliyonse yamumlengalenga, fano la chilichonse chokwaŵa pa nthaka, ndi fano la nsomba iliyonse yam'madzi pansi pa dziko. Musamale kuti mukapenya ku thambo nkuwona dzuŵa, mwezi, nyenyezi ndi zonse zakuthamboko, mtima wanu usakopeke nkuyamba kupembedza ndi kutumikira zinthu zimene Mulungu wanu wapatsa anthu ena onse a pa dziko lapansi. Koma inu ndinu anthu amene Mulungu adakutulutsani ku dziko la Ejipito, ng'anjo yotentha ija. Adakutulutsanimo kuti mukhale anthu akeake monga m'mene muliri leromu. Chauta, Mulungu wathu, adandikwiyira ine chifukwa cha inu. Ndipo adalumbira kuti ine sindiwoloka mtsinje wa Yordani kukaloŵa m'dziko lokoma limene akukupatsanilo ngati choloŵa chanu. Ndidzafera m'dziko lomwe lino osaoloka mtsinjewo. Koma inu, muli pafupifupi kuwoloka ndi kukhala m'dziko lokomalo. Samalani bwino, musaiŵale chipangano chimene Chauta, Mulungu wanu, adachita nanu, ndipo musapange fano lofanizira chinthu chilichonse chimene Chauta, Mulungu wanu, adakuletsani. Paja Chauta, Mulungu wanu, ndi Mulungu wansanje, salola kuti wina apikisane naye. Ali ngati moto waukali. Ngakhale mutakhala m'dzikomo nthaŵi yaitali, ndi kubereka ana ndi zidzukulu, musadzachimwe pakudzipangira fano la maonekedwe ena aliwonse. Pamaso pa Chauta ndi zoipa zimenezi, ndipo adzapsa nazo mtima. Mukachita zimenezi, ndikukuuzani lero, kumwamba ndi dziko lapansi zikhale mboni, kuti simudzakhalitsa pa dziko. Mudzaonongeka m'dziko ili la patsidya pa Yordani, limene mukukakhalamolo. Mudzaonongeka nonsenu. Chauta adzakumwazani pakati pa mitundu ina, ndipo oŵerengeka okha mwa inu ndiwo adzatsala pakati pa mitundu ina kumene Chauta adzakupirikitsirani. Kumeneko muzidzatumikira milungu yopanga ndi manja, monga yamtengo ndi yamwala, milungu imene singathe kupenya kapena kumva, kudya kapenanso kununkhiza. Kumeneko inu mudzafunafuna Chauta, Mulungu wathu, ndipo ngati mudzamfunafuna ndi mtima wonse ndi moyo wanu wonse, mudzampeza. Mukadzakhala pa mavuto, ndipo zinthu zonsezi nkukuchitikirani, pamenepo mudzabwerera kwa Chauta, Mulungu wanu, ndipo mudzamvera mau ake. Paja Chauta, Mulungu wanu, ndi Mulungu wachifundo. Sadzakulekererani kapena kukuwonongani. Chipangano chimene Iye adachita molumbira ndi makolo anu, sadzachiiŵala. Tafufuzani zakale, inu musanabadwe, kuyambira pa tsiku lija limene Mulungu adalenga munthu pa dziko lapansi. Tafufuzani pa dziko lonse lapansi. Kodi chachikulu chonga chimenechi chidachitikapo ndi kale lonse? Kodi alipo wina amene adamvapo zotere? Kodi alipo anthu ena amene adakhalabe ndi moyo, atamva mau a Mulungu ali m'moto, monga m'mene mudamvera inu? Kodi alipo mulungu wina aliyense amene adaapita kukadzitengera anthu kuŵachotsa pakati pa fuko lina, naŵasandutsa anthu akeake, monga muja Chauta, Mulungu wanu, adakuchitirani inu ku Ejipito kuja? Iye adachita zimenezo ndi mphamvu zake zazikulu, inu mukupenya. Adadzetsa miliri pamodzi ndi nkhondo, adachita zozizwitsa ndi zodabwitsa. Chauta adakuwonetsani zimenezi, kuti inu mudziŵe kuti Chauta yekha ndiye Mulungu, ndipo kuti palibenso wina. Chauta adalola kuti mumve mau ake kuchokera kumwamba, kuti pakutero akuphunzitseni. Pa dziko lapansi pano Chauta adakuwonetsani moto waukulu, ndipo mudamva akulankhula nanu kuchokera m'motomo. Popeza kuti Chauta adakonda makolo anu, adasankha inu zidzukulu zao nakutulutsani ku Ejipito pakuwonetsa ulemu ndi mphamvu zake zazikulu. Pamene munkayenda, Iye adapirikitsira kutali mitundu ikuluikulu kupambana inu, kuti akuloŵetseni ndi kukupatsani dziko laolo, kumene muli lero lino. Choncho dziŵani ndipo musamaiŵala kuti Chauta ndiye Mulungu wa kumwamba ndi wa dziko lapansi, palibe wina ai. Muzimvera malangizo ndi malamulo ake onse amene ndakupatsani leroŵa. Mukatero, zinthu zidzakuyenderani bwino inuyo ndi zidzukulu zanu, ndipo mudzakhalitsa m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, adzakupatsani kuti likhale lanu mpaka muyaya. Pamenepo Mose adapatula mizinda itatu kuvuma kwa Yordani kumene munthu wopha mnzake mwangozi, osati mwachidani, ankatha kuthaŵirako ndi kupulumutsa moyo wake. A fuko la Rubeni, mzinda wao unali Bezeri umene unali m'chipululu, m'dziko lamapiri. A fuko la Gadi, mzinda wao unali Ramoti umene unali m'dziko la Giliyadi. Ndipo a fuko la Manase mzinda wao unali Golani umene unali m'dziko la Basani. Aŵa ndi malamulo amene Mose adapatsa Aisraele. Ameneŵa ndi malamulo ndi mau ndiponso malangizo amene Mose adauza Aisraele, atatuluka ku Ejipito. Aisraelewo anali m'chigwa kuvuma kwa mtsinje wa Yordani, kuyang'anana ndi mudzi wa Betepeori. Kumeneko ndi dziko la Sihoni, mfumu ya Aamori, amene ankalamula mzinda wa Hesiboni, ndipo Mose ndi Aisraelewo atatuluka m'dziko la Ejipito, adamgonjetsa Sihoniyo. Aisraele aja adakakhala m'dziko lake ndi m'dziko la mfumu Ogi wa ku Basani. Ameneŵa anali mafumu aŵiri a Aamori amene ankakhala kuvuma kwa Yordani. Dziko limene adalandalo lidayambira ku mudzi wa Aroere pamphepete pa mtsinje wa Arinoni, mpaka kukafika ku phiri la Sirioni (ndiye kuti phiri la Heremoni), ndi dziko lonse la Araba la kuvuma kwa mtsinje wa Yordani, mpaka kukafika ku Nyanja ya Araba, patsinde pa phiri la Pisiga. Mose adaitana Aisraele onse naŵauza kuti: Inu Aisraele, mverani malamulo ndi malangizo onse amene ndikukupatsani lero. Muŵaphunzire, ndipo musamaledi kuti muzimvera. Chauta, Mulungu wathu, adachita nafe chipangano pa phiri la Horebu. Sikuti chipangano chimenechi adangochita ndi makolo athu okha ai, komanso ndi ife tonse amene tili ndi moyo pano lero lino. Mulungu adalankhula nanu pamasompamaso, kuchokera m'moto paphiri paja. Nthaŵi imene ija, ine ndidaaima pakati pa inu ndi Chauta ndi kumakuuzani mau a Chauta, chifukwa inu munkaopa moto, ndipo simudakwere phiri. Chauta adaati, “Ine ndine Chauta, Mulungu wako, amene ndidakutulutsa iwe ku Ejipito, dziko laukapolo. “Usapembedze Mulungu wina, koma Ine ndekha. “Usadzipangire fano kufanizira kanthu kolengedwa kalikonse kakumwamba, kapena ka pa dziko lapansi, kapena ka m'madzi a pansi pa dziko. Usagwadire fano lililonse kapena kulipembedza, chifukwa Ine, Chauta, Mulungu wako, ndine Mulungu wansanje, sindilola kuti wina apikisane nane. Ndimalanga amene adana nane. Ndimalanganso zidzukulu zao, mpaka mbadwo wachitatu ndi wachinai. Koma ndimachitira chifundo chosasinthika anthu zikwi zambirimbiri amene amandikonda namasunga malamulo anga. “Usatchule pachabe dzina la Chauta, Mulungu wako, chifukwa Chauta adzamlanga aliyense wotchula pachabe dzina lakelo. “Uzisunga tsiku la Sabata ndi kuliyeretsa, monga momwe Ine Chauta, Mulungu wako, ndidakulamulira. Uzigwira ntchito zako zonse ndi kuzitsiriza pa masiku asanu ndi limodzi. Koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi la Sabata la Chauta, Mulungu wako. Pa tsiku limenelo, usagwire ntchito iliyonse iweyo, mwana wako wamwamuna, mwana wako wamkazi, wantchito wako wamwamuna, mdzakazi wako, ng'ombe yako, bulu wako, kaya choŵeta chako chilichonse, ngakhale mlendo wokhala m'mudzi mwako. Motero atumiki ako aamuna ndi aakazi azipumanso monga iwe wemwe. Uzikumbukira kuti paja udaali kapolo m'dziko la Ejipito, ndipo kuti Ine Chauta, Mulungu wako, ndidakutulutsako ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasula. Nchifukwa chake Chauta, Mulungu wako, adakulamula kuti uzisunga tsiku la Sabata ndi kuliyeretsa. “Uzilemekeza atate ako ndi amai ako, monga momwe Chauta, Mulungu wako, adakulamulira, kuti pakutero masiku a moyo wako achuluke ndipo kuti zinthu zikuyendere bwino m'dziko limene Chauta, Mulungu wako, akukupatsa iwe. “Usaphe. “Usachite chigololo. “Usabe. “Usamchitire mnzako umboni wonama. “Usasirire mkazi wa mnzako. Usasilire nyumba yake, munda wake, wantchito wake wamwamuna, wantchito wake wamkazi, ng'ombe yake, bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzakoyo.” Chauta adaalankhula mau ameneŵa kwa inu nonse amene mudaasonkhana kuphiri kuja. Iye adanena mau ameneŵa osaonjezerapo kanthu, ndipo adalankhula mau amphamvu, kuchokera m'moto, m'mitambo ndiponso mu mdima wandiweyani. Pambuyo pake adalemba malamulo khumiwo pa miyala iŵiri, ndipo adandipatsa ine. Pamene mudamva mau ochokera mu mdima, phiri lonse likuyaka moto, atsogoleri anu pamodzi ndi mafumu a mabanja anu adabwera kwa ine, ndipo adati, “Chauta, Mulungu wathu, adatiwonetsa ukulu ndi ulemerero wake, ndipo tidamumva akulankhula m'moto muja. Lero taona kuti munthu angathe kukhalabe ndi moyo ndithu, ngakhale kuti Mulungu walankhula naye. Koma ife, tiferenji kuno? Moto woopsawo udzatiwononga. Tidzafa tikamva Chauta, Mulungu wathu, akulankhulanso. Kodi alipo wina aliyense amene adakhalapo ndi moyo atamva Mulungu wamoyo akulankhula m'moto monga momwe tidamvera ifeyo? Inu Mose, musendere, ndipo mukamvere zonse zimene Chauta, Mulungu wathu, adzanene. Kenaka mubwere, mudzatiwuze tonsefe zimene wakuuzani inuyo. Ife tidzamvera ndipo tidzachita.” Pamene mudalankhula ndi ine, Chauta adamva mau anu ndipo adandiwuza kuti, “Ndamva zimene akulankhula anthuzi, ndi zabwino zokhazokha zonsezo. Ine ndikufuna kuti aziganiza zimenezo masiku onse. Ndikufuna kuti azindiwopa nthaŵi zonse, ndipo kuti azimvera malamulo anga, kuti zinthu ziŵayendere bwino iwowo ndi zidzukulu zao mpaka muyaya. Uŵauze kuti abwerere ku mahema ao. Koma iwe Mose, ukhale kuno pamodzi ndi Ine, ndipo ndidzakupatsa malamulo, malangizo ndi zina zoyenera kuzitsata. Zonsezi ukaŵaphunzitse anthu kuti azikasunga malamulowo m'dziko limene ndidzaŵapatsalo.” Inu Aisraele, musamale ndithu kuchita zimene Chauta, Mulungu wanu, wakulamulani, osapatukira ku dzanja lamanja kapena lamanzere. Muziyenda m'njira imene Chauta, Mulungu wanu, wakulamulani, kuti zinthu zidzakuyendereni bwino, ndipo mudzapitirire kukhala ndi moyo m'dziko limene mukakhalemolo. Tsono aŵa ndi malamulo, malangizo ndi zina zoyenera kuzitsata, zimene Chauta, Mulungu wanu, adandilamula kuti ndikuphunzitseni. Muzikatsata zonsezi m'dziko limene mudzaloŵa ndi kukhalamolo, nthaŵi zonse pamene muli moyo, inu ndi zidzukulu zanu. Muzikaopa Chauta, Mulungu wanu, ndipo muzikamvera malamulo ndi malangizo ake onse amene ndikukupatsaniŵa, kuti pakutero mukakhale moyo nthaŵi yaitali. Inu Aisraele, mutchere khutu, ndipo muchenjere, mumveredi malamuloŵa. Tsono zinthu zidzakuyenderani bwino, ndipo mudzakhala mtundu wochuluka zedi ndi kumakhala m'dziko lamwanaalirenji, monga momwe Chauta, Mulungu wa makolo anu, adakulonjezerani. Mverani, inu Aisraele, Chauta Mulungu wathu ndi mmodzi yekha. Muzikonda Chauta, Mulungu wanu, ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse ndi mphamvu zanu zonse. Muziŵasunga bwino mumtima mwanu malamulo amene ndikukupatsani leroŵa. Muziŵaphunzitsa mwachangu kwa ana anu kulikonse kumene muli, mutakhala pansi m'nyumba mwanu, kapena muli paulendo, kapena mukupumula, kapena mukugwira ntchito. Amangeni pamikono panu, ndiponso muŵaike pa mphumi pakati pa maso anu. Alembeni pa mphuthu za zitseko za nyumba zanu ndi pa zipata zanu. Chauta, Mulungu wathu, adalonjeza makolo anu aja Abrahamu, Isaki ndi Yakobe kuti adzakupatsani inu dziko limene lili ndi mizinda ikuluikulu ndi yachuma, imene inu simudaimange. Nyumba zake zidzakhala zodzaza ndi zinthu zabwino zimene inuyo simudaikemo. Zitsime zidzakhala zokumbiratu ndipo padzakhala minda yamphesa ndi yaolivi imene simudalime ndinu. Chauta akadzakuloŵetsani m'dziko limeneli, ndipo mukadzakhala ndi chakudya chambiri, musadzaiŵale Chauta amene adakutulutsani ku Ejipito, dziko laukapolo. Muziwopa Chauta, Mulungu wanu. Muzipembedza Iye yekha, ndipo mukamalumbira, muzitchula dzina lake lokha. Musamapembedza milungu ina, milungu imene amaipembedza anthu okhala mozunguliramu, popeza kuti mukatero, mkwiyo wa Chauta udzakuyakirani ngati moto, ndipo udzakuwonongani kwathunthu, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, amene amakhala pakati panu, ndi Mulungu wansanje, salola kuti wina apikisane naye. Musamupute Chauta, Mulungu wanu, monga mudachitira ku Masa kuja. Musamale kuti musunge malamulo onse amene Iye akupatsani. Muzichita zokhazo zimene Chauta akuti ndi zolungama ndi zabwino, ndipo zinthu zidzakuyenderani bwino. Mudzalandira dziko labwinolo limene Chauta adalonjeza molumbira kuti adzapatsa makolo anu. Adani anu mudzaŵapirikitsa, monga Chauta adalonjezera. Nthaŵi zakutsogoloko, ana anu adzakufunsani kuti, “Kodi chifukwa chiyani Chauta, Mulungu wathu, adakulamulani kuti muzimvera malamulo ndi malangizo ndi zina zonse zoyenera kuzitsatazi?” Tsono inu mudzaŵauze kuti, “Ife tidaali akapolo a mfumu ya dziko la Ejipito, koma Mulungu adatipulumutsa ndi mphamvu zake zazikulu. Ife tidapenya ndi maso athu Chauta akuchita zodabwitsa ndi zoopsa kuti alange Aejipito, mfumu yao ndi banja lao lonse. Mulunguyo adatitulutsa ife ku Ejipito, natifikitsa kuno ndi kutipatsa dziko lino, monga momwe adalonjezera kwa makolo athu. Pamenepo Mulungu wathu adatilamula kuti tizimvera malamulo onseŵa, ndiponso kuti tizimuwopa. Tikamatero, Iyeyo adzasunga mtundu wathu, ndipo adzautukula monga momwe akuchitiramu tsopano. Tikamasunga mokhulupirika zonse zimene Chauta Mulungu wathu watilamula, Iyeyo adzakondwera nafe.” Chauta, Mulungu wanu, adzakufikitsani m'dziko limene mukudzakhalamolo, ndipo mitundu ina yonse ya anthu adzaipirikitsa m'dzikomo. Iye adzachotsamo mitundu isanu ndi iŵiri ya anthu otchuka ndi amphamvu kupambana inu. Mitunduyo ndi iyi: Ahiti, Agirigasi, Aamori, Akanani, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi. Chauta, Mulungu wanu, akadzapereka anthu ameneŵa kwa inu ndipo mukadzaŵagonjetsa, mudzaŵaononge onsewo. Musakayanjane nawo, kapena kuŵachitira chifundo. Musakakwatirane nawo, ndiye kuti musakalole ana anu kukwatirana nawo, kuti angadzaŵasokeretse kuŵachotsa kwa Chauta, Mulungu wanu, namakapembedza nawo milungu ina. Mukadzatero, Chauta adzakukwiyirani, ndipo adzakuwonongani mwamsanga. Anthu amenewo mudzaŵachite izi: mudzaphwanye maguwa ao, mudzaphwanye miyala yoimiritsa yopembedzapo, mudzagwetse mafano ao aja a Aserimu, ndipo mudzatenthe mafano ao osema. Inu ndinu mtundu wopatulika wa Chauta, Mulungu wanu. Mulungu adasankha inu kuti mukhale anthu ake pakati pa anthu onse a pa dziko lapansi. Mulungu pokukondani ndi kukusankhani inu, sadachitire kuti munkaposa anthu ena onse pakuchuluka. Paja mudaali ochepa ndinuyo pakati pa mitundu yonse. Koma Chauta adakukondani, ndipo adafunadi kusunga malumbiro amene adaachita ndi makolo anu. Nchifukwa chake adakupulumutsani ndi mphamvu zake, nakusandutsani mfulu, kukuchotsani m'dziko laukapolo kwa mfumu ya ku Ejipito ija. Nchifukwa chake mudziŵe kuti Chauta, Mulungu wanu, ndiye yekha Mulungu, ndipo ndi Mulungu wokhulupirika. Iye adzasungadi chipangano chake ndipo adzaonetsa chifundo chake chosasinthika kwa anthu a mibadwo zikwi zambirimbiri amene amakonda Iye namamvera malamulo ake. Koma onse amene amadana ndi Mulungu, adzaŵabwezera pakuŵaononga. Sadzamlekerera munthu wodana naye, koma adzamubwezera pakumlanga ndithu. Motero, muzimvera mosamala malangizo ndi malamulo amene ndikukulamulani leroŵa. Ngati mumvera ndi kutsata mokhulupirika malamulo onse mwamvaŵa, Chauta, Mulungu wanu, adzapitirirabe kusunga chipangano chake chimene adachita ndi inu, ndipo adzapitiriranso kukukondani, monga momwe adalonjezera makolo anu. Adzakukondani ndi kukudalitsani, kotero kuti mudzachuluka ndi kubereka ana ambiri. Minda yanu adzaidalitsa, kotero kuti tirigu, vinyo ndi mafuta, mudzakhala nazo zonsezo. Adzakudalitsaninso pa zoŵeta pokupatsani ng'ombe zambiri ndi zoŵeta zina zomwe. Madalitso onseŵa, adzakupatsani muli m'dziko limene adalonjeza makolo anu. Pa dziko lapansi, palibe anthu amene adzakhale odala ngati inu. Sipadzaoneka mwamuna kapena mkazi wosabala pakati panu, ndiponso pakati pa zoŵeta zanu. Chauta adzakutchinjirizani pa matenda onse. Iye sadzalolanso kuti matenda oopsa a ku Ejipito amene mumaŵadziŵa aja, afikenso pa inu, koma Mulungu adzadzetsa matenda ameneŵa pa adani anu onse. Mitundu yonse imene Chauta, Mulungu wanu, aipereke kwa inu, muiwononge mopanda chifundo. Musapembedze milungu yao, popeza kuti kuteroko nkugwa mu msampha. Musanene kuti anthu ameneŵa achuluka kupambana inu, ndipo kuti simungathe kuŵapirikitsa. Musaŵaope. Kumbukirani zimene Chauta, Mulungu wanu, adam'chita Farao mfumu ya ku Ejipito, pamodzi ndi anthu ake omwe. Kumbukirani miliri yoopsa ija imene mudaiwona ndi maso anu. Mudaona zozizwitsa ndi zodabwitsa zomwe, ndiponso zinthu zazikulu zamphamvu. Zimenezi Chauta, Mulungu wanu, adazichita ndi dzanja lake lamphamvu, kuti akumasuleni. Anthu onse amene mumaŵaopaŵa, Chauta Mulungu wanu adzaŵaononga monga momwe adaonongera Aejipito. Ndiponsotu adzatumiza mliri wa mavu pakati pao, umene udzaononga onse othaŵa ndi obisala. Musaŵaope anthu ameneŵa. Chauta Mulungu wanu ali nanu. Iyeyo ndiye Mulungu wamkulu woyeneradi kumuwopa. Inu mukamayenda, Iye adzapirikitsa mitundu imeneyi pang'onopang'ono. Komatu simudzaŵatha onse nthaŵi imodzi. Mukadatero, nyama zakuthengo zikadachuluka ndi kumakuwopsani. Chauta adzapereka adani anuwo kwa inu, ndipo adzaŵasokoneza kwambiri mpaka atatha onse. Mafumu onse adzaŵapereka kwa inu. Mudzaŵapha onse, ndipo adzaiŵalika. Palibe amene adzakuletseni, mpaka mudzaŵaononga onsewo. Mudzatenthe mafano ao ofanizira milungu yao. Musadzakhumbire siliva kapena golide amene iwo adapangira mafanowo. Musadzatengeko zimenezi kuti mungagwe mu msampha, popeza kuti zimenezo zimamnyansa Chauta, Mulungu wanu. Musadzaloŵe nazo m'nyumba mwanu zimenezi, kuti tsoka limene lili pa iwowo lingadzakhale pa inu. Mudzadane ndi mafanowo ndi kuŵanyoza, chifukwa Chauta adaŵatemberera. Zonse zimene ndakulamulani lero, mumvere mokhulupirika, kuti mukhale ndi moyo, muchulukane, ndipo mukakhazikike m'dziko limene Chauta adalonjeza makolo anu. Kumbukirani m'mene Chauta, Mulungu wanu, adakutsogolerani m'chipululu, pa ulendo wa pa zaka zonse makumi anai zapitazi. Adakuvutani nakuyesani ndi zoŵaŵa, kuti adziŵe zimene zinali m'mitima mwanu, ndipo kuti aone ngati mudzamvera malamulo ake kapena ai. Adakutsitsani pokukhalitsani ndi njala, komanso adakupatsani mana kuti mudye. Inu ndi makolo anu simudadyepo ndi kale lonse chakudya chimenechi. Adachita zimenezi kuti akuphunzitseni kuti munthu sakhala ndi moyo ndi chakudya chokha ai, koma ndi mau onse otuluka m'kamwa mwa Mulungu. Zovala zanu sizidathe, ndipo ngakhale mapazi anu omwe sadatupe konse m'chipululu pa zaka makumi anai zonsezi. Dziŵani kuti Chauta, Mulungu wanu, amakulangani monga momwe bambo amalangira ana ake. Tsono inu, muzichita monga momwe Chauta akulamulirani. Muziyenda m'njira zake ndipo muzimuwopa. Chauta, Mulungu wanu, adzakuloŵetsani m'dziko lokoma, dziko la mitsinje, la zitsime, la akasupe otumphukira m'zigwa ndi m'mapiri. Lilinso ndi tirigu, barele, mphesa, nkhuyu, makangaza, olivi ndi uchi. Kumeneko simudzakhala ndi njala, ndipo simudzasoŵa kanthu. Zitsulo zimapezeka m'miyala ya kumeneko, ndipo mungathe kukumbamo mkuŵa m'mapiri mwake. Mudzakhala ndi chakudya chokwanira ndipo mudzakhuta, tsono mudzathokoza Chauta, Mulungu wanu, chifukwa wakupatsani dziko lokoma. Samalani kuti musamaiŵala Chauta, Mulungu wanu. Musamalephera kumvera malamulo ndi malangizo ake amene ndakupatsani leroŵa. Mukadzadya ndi kukhuta, mukadzamanga nyumba zabwino zoti mudzakhalemo, mukadzakhala ndi ng'ombe, nkhosa, siliva ndi golide, ndipo chuma chanu chikadzanka chiwonjezekeraonjezekera, pamenepo musadzanyade ndi kuiŵala Chauta, Mulungu wanu, amene adakutulutsani ku Ejipito kumene mudaali akapolo. Iye adakutsogolerani, mpaka mudabzola chipululu chachikulu ndi choopsa chija, m'mene munali njoka za ululu woopsa ndi zinkhanira. Adakupatsani madzi otuluka m'thanthwe, m'dziko louma lopanda madzi lija. Adakupatsani mana oti mudye, chakudya chimene makolo anu anali asanadyepo, pofuna kukutsitsani ndi kukuyesani, kuti pambuyo pake akuchitireni zokoma. Tsono muchenjere, musamati, “Ndapeza chuma chonsechi ndi mphamvu zanga ndi nyonga zanga.” Kumbukirani kuti amene amakupatsani mphamvu zoti mulemerere, ndi Chauta, Mulungu wanu. Adachita zimenezi kale popeza kuti sadafune kuphwanya chipangano chake chimene adachita ndi makolo anu, chimodzimodzi m'mene akuchitira lero. Musamuiŵale Chauta, Mulungu wanu, ndi kutembenukira kwa milungu ina kuti muipembedze. Mukachimwa motero, ndithudi mudzaonongeka. Mukapanda kumvera Chauta, Mulungu wanu, mudzaonongeka monga momwe Chauta akuwonongera mitundu ina pamaso panu. Mvetsani inu Aisraele. Muli pafupi kuwoloka mtsinje wa Yordani ndi kukakhala m'dziko la anthu aakulu ndi amphamvu kupambana inu. Mizinda yao ndi ya malinga aatali ofika mpaka kumwamba. Anthu ake ngotchuka ndiponso ataliatali. Anthu amenewo ndi zidzukulu za Aanaki amene mukuŵadziŵa kale. Paja mudamva kale kuti amati, “Ndani angalimbane ndi zidzukulu za Anaki?” Koma lero mudziŵe kuti Chauta, Mulungu wanu, ndiye amene adzakutsogolerani monga momwe umachitira moto wopsereza. Adzagonjetsa onse pamaso panu, kotero kuti mudzaŵapirikitsa ndi kuŵaononga mwamsanga monga Chauta adakulonjezerani. Chauta, Mulungu wanu, ndiye adzakupirikitsirani iwowo. Ndiye inu musadzanene kuti wakuloŵetsani ndi kukupatsani dzikolo chifukwa cha zabwino zimene mwachita. Ai, Chauta akupirikitsirani anthu ameneŵa chifukwa choti iwowo ngoipa. Chimene Chauta akukulolerani kuŵalanda dziko anthuwo, si chifukwa chakuti ndinu abwino ndi angwiro ai. Akuŵapirikitsa chifukwa iwowo ngoipa, ndiponso chifukwa choti Mulungu ndi wosunga lonjezo limene adachita ndi makolo anu Abrahamu, Isaki ndi Yakobe. Mudziŵe tsono kuti Chauta sakukupatsani dziko labwinoli popeza kuti ndinu olungama ai. Inu ndinu anthu okanika. Musaiŵale m'mene mudakwiyitsira Chauta, Mulungu wanu, m'chipululu muja. Kuyambira tsiku lija mudatuluka ku Ejipito kuja, mpaka tsiku limene mudafika kuno, mwakhala mukuukira Chauta, Mulungu wanu. Ngakhale ku phiri la Horebu kuja, mudakwiyitsa Chauta, kukwiya kwake koti akadakuwonongani. Ine ndidakwera phiri kukalandira miyala iŵiri imene padalembedwapo chipangano chimene Chauta adachita nanu. Ndidakhala kumeneko masiku makumi anai, usana ndi usiku, ndipo sindidadye kapena kumwa kanthu kalikonse. Tsono Chauta adandipatsa miyala iŵiri ija imene Iye yemwe adaalembapo ndi dzanja lake zonse zimene adalankhula ndi inu ali m'moto, pa tsiku lija mudasonkhana kuphiri kuja. Zedi, patapita masiku makumi anaiwo, usana ndi usiku, Chauta adandipatsa miyala iŵiri ija, imene adaalembapo chipangano. Pamenepo Chauta adandiwuza kuti, “Nyamuka tsika msanga, choka kuphiri kuno, chifukwa anthu ako aja udaŵatsogolera kuchokera ku Ejipitoŵa, adziipitsa kwambiri. Sadakhalire kupatuka pa zimene ndidaŵalamula kuti azichita, ndipo adzipangira fano losungunula.” Chauta adandiwuzanso kuti, “Anthuŵa ndikuŵadziŵadi, ndi anthu okanika. Usandiletse, ndikufuna kuŵaononga ndi kufafaniziratu dzina lao pansi pa thambo. Koma iwe ndidzakusandutsa mtundu waukulu ndi wamphamvu kupambana iwoŵa.” Pomwepo ndidatsika phiri, nditanyamula m'manja mwanga miyala iŵiri ija ya chipangano. M'phirimo munkatuluka malaŵi a moto. Nditayang'ana, ndidaona kuti inu mudachimwira Chauta, Mulungu wanu, pakudzipangira fano lachitsulo la mwanawang'ombe. Simudakhalire kuleka kusunga malamulo amene Chauta adakulamulani. Pompo ine ndidaponya pansi miyalayo ndi kuiswa, inu mukuwona. Tsono masiku enanso makumi anai, usana ndi usiku, ndidagwada pamaso pa Chauta ndipo ndidapemphera. Sindidadye kapena kumwa kanthu kalikonse, chifukwa inuyo mudaachimwira Chauta ndikumkwiyitsa. Ine ndinkaopa mkwiyo wa Chauta woopsawo, chifukwa kukwiya kwake kunali koti akadakuwonongani. Koma nthaŵi imeneyo Chauta adamvanso pemphero langa. Chauta adakwiyiranso Aroni, kotero kuti akadamupha ndithu, koma ndidampemphereranso nthaŵi yomweyo. Chinthu chimene mudachipangacho, fano lachitsulo la mwanawang'ombelo, ndidaliponya pa moto. Tsono ndidaliphwanya pafupipafupi ndi kuliperapera, ndipo ndidataya phulusa lake ku mtsinje wotsika m'phiri uja. Inu mudakwiyitsanso Chauta, Mulungu wanu, pamene munali ku Tabera, ku Masa ndi ku Kibroti-Hatava. Ndipo Chauta atakutumani kuchokera ku Kadesi-Baranea kuti mupite kukalandira dziko limene adakupatsanilo, inu mudakana malamulo a Chauta, Mulungu wanu, ndipo simudamkhulupirire kapena kumumvera. Mwakhala mukumuukira Chauta kuyambira pamene ine ndidakudziŵani. Motero ndidagwada pamaso pa Chauta ndipo ndidapemphera masiku makumi anai, usana ndi usiku, chifukwa Chauta adaatsimikiza zokuwonongani. Ndidapemphera motere, ndidati, “Inu Chauta, Ambuye athu, chonde musaŵaononge anthuŵa amene mudaŵasankha kuti akhale anuanu. Anthu ameneŵa mudaŵapulumutsa ndi ukulu wanu ndipo mudaŵatulutsa ku Ejipito ndi mphamvu zanu zazikulu. Kumbukirani atumiki anu aja, Abrahamu, Isaki ndi Yakobe, ndipo musasamale kukanika kwa anthu anuŵa, kuipa kwao ndi kuchimwa kwao, kuti Aejipito aja angamadzanene kuti Inu simudathe konse kuŵaloŵetsa anthu anu m'dziko limene mudaŵalonjeza. Azidzanenanso kuti: Adaŵatulutsa anthuwo kuti akaŵaphe ku chipululu poti adadana nawo. Chonsecho anthu ameneŵa mudaŵasankha kuti akhale anuanu, ndipo mudaŵatulutsa ku Ejipito ndi mphamvu zanu zazikulu ndi mkono wanu wotambalitsa.” Nthaŵi yomweyo Chauta adandiwuzanso kuti, “Semani miyala iŵiri monga yoyamba ija, ndipo upange bokosi lamtengo kuti uziikamo miyalayo, tsono ukwere kuphiri kuno kwa Ine. Ndipo pa miyala imeneyi ndidzalembapo zomwe ndidaalemba pa miyala yoyamba udaphwanya ija, tsono ukaike miyala imeneyi m'bokosimo.” Pompo ndidapanga bokosi la mtengo wakasiya, ndipo ndidasemanso miyala iŵiri monga yoyamba ija, ndipo ndidakwera phiri, nditatenga miyalayo. Pamenepo Chauta adalemba pa miyalayo mau omwewo amene adaalemba pa miyala ija. Mauwo ndiwo malamulo khumi amene adakupatsani pamene adalankhula nanu m'moto muja, pa tsiku limene mudasonkhana nonse kuphiri kuja. Chauta adandipatsa miyalayo, ndipo ndidatembenuka ndi kutsika phirilo. Tsono monga momwe Chauta adalamulira, ndidatsekera miyalayo m'bokosi limene ndidaapanga, ndipo ili m'menemo. (Aisraele adachoka ku Beeroti-Bene-Yaakani, napita ku Mosera. Aroni atamwalira adaikidwa komweko. Mwana wake Eleazara ndiye amene adaloŵa m'malo mwake, kukhala wansembe. Kuchokera kumeneko, Aisraele adapita ku Gudigoda napitirira mpaka ku Yotibata, dziko la mtsinje ya madzi ambiri. Nthaŵi imeneyo Chauta adasankha a fuko la Levi, kuti azinyamula Bokosi lachipangano, azikhala pamaso pa Chauta ndi kumatumikira, ndiponso kuti azidalitsa anthu m'dzina la Chauta. Ndiwo amene amachita zimenezi mpaka lero lino. Nchifukwa chake fuko la Levi silidalandireko dziko kapena choloŵa monga mafuko ena aja. Chauta ndiye choloŵa chao, monga momwe Chauta, Mulungu wanu, adalonjezera.) Ine ndidakhala paphiripo masiku makumi anai, usana ndi usiku, monga momwe ndidaachitira nthaŵi yoyamba ija. Chauta adandimveranso nthaŵi imeneyi navomera kuti sadzakuwonongani. Tsono adandiwuza kuti ndipite nanu, ndikhale mtsogoleri wanu, kuti potero muloŵe ndi kukhazikika m'dziko limene Iye adalumbira kuti adzapatsa makolo anu. Tsono inu Aisraele, tamvani zimene Chauta, Mulungu wanu, akukuuzani. Akufuna kuti muzimuwopa ndi kuchita zonse zimene amakulamulani. Muzikonda Chauta, ndipo muzimtumikira ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, ndipo muzimvera malamulo ndi malangizo onse a Chauta amene ndikukulamulani lero lino, kuti zinthu zikukomereni. Kumwamba ndi zonse zili kumeneko ndi zake za Chauta, pamodzi ndi dziko lapansi pano ndi zonse zili m'menemo. Komabe Chauta adakonda makolo anu kwambiri, kotero kuti m'malo mwa kusankha anthu ena, adasankha zidzukulu za makolo anuwo, ndiye kuti inuyo, mpaka lero lino. Tsono muchotse zoipa m'mitima mwanu, ndipo mulekeretu kukhala ndi mtima wokanika. Pakuti Chauta, Mulungu wanu, ndi Mulungu wopambana milungu yonse, ndiponso ndi Ambuye oposa ambuye onse. Ndi wamkulu, wamphamvu ndi woopsa, sakondera, ndipo salandira ziphuphu. Amateteza ana amasiye ndi akazi amasiye. Amakonda anthu achilendo amene amakhala pakati panu, ndipo amaŵapatsa chakudya ndi zovala zomwe. Tsono muŵakonde anthu achilendowo, chifukwa paja inunso mudaali alendo ku Ejipito. Muzimvera Chauta, Mulungu wanu, ndipo muzipembedza Iye yekha. Muzikhala okhulupirika kwa Iyeyo ndipo muzilumbira m'dzina lake lokha. Mtamandeni pakuti ndiye Mulungu wanu, ndipo mwadziwonera nokha zinthu zazikulu ndi zoopsa zimene adakuchitirani. Pamene makolo anu ankapita ku Ejipito, adaalipo makumi asanu ndi aŵiri okha. Koma tsopano Chauta, Mulungu wanu, wakuchulukitsani ngati nyenyezi zamumlengalenga. Muzikonda Chauta, Mulungu wanu, ndipo nthaŵi zonse muzimvera malamulo ndi malangizo ake onse. Popeza kuti si ana anu, koma ndinu amene mudazidziŵa ndi kuziwona zakale zonsezo, mukumbukire za Chauta, Mulungu wanu. Ukulu wake mudauwona, mudaonanso dzanja lake lamphamvu ndi mkono wake wotambalitsa. Mudaona zizindikiro ndi ntchito zimene Chauta adachita polanga Farao ndi dziko lake lonse. Mudaona zimene adachita polimbana ndi ankhondo a ku Ejipito ndiponso ndi akavalo ndi magaleta ao. Pamene iwo ankathamangitsa inu, mudaona m'mene Chauta adalamulira madzi a Nyanja Yofiira kuti aŵaphimbe ndi kuŵaononga onsewo. Mudaona zonse zimene Chauta adakuchitirani m'chipululu muja, musanafike kuno. Mudaona zimene Chauta adachita pa Datani ndi pa Abiramu, ana a Eliyabu, a fuko la Rubeni. Pamaso pa Aisraele onse nthaka idatsekuka nkuŵakwirira anthuwo, pamodzi ndi a m'banja mwao, mahema ao ndi zoŵeta zao zomwe. Zoonadi mudaona zazikulu zonse zimene Chauta adachita. Muzimvera zonse zimene ndakulamulani lerozi. Tsono mukatero, mudzakhala amphamvu, ndipo mudzaloŵa ndi kukhazikika m'dzikomo. Mudzakhaladi nthaŵi yaitali m'dziko lamwanaalirenjilo, limene Chauta adalumbira kuti adzapatsa makolo anu ndi zidzukulu zao. Dziko limene mukukakhalamolo likusiyana ndi dziko la Ejipito kumene mudachokera. Kumene kuja munkati mukafesa mbeu zanu, munkachita kuthirira ngati m'madimba. Koma dziko limene mukukaloŵamolo ndi lamapiri ndi lazigwa. M'dziko limenelo mvula siitha. Chauta, Mulungu wanu, ndiye amene amasamalira dziko limenelo ndi kumaliyang'anira chaka chonse mosalekeza. Nchifukwa chake tsono muzimvera malamulo ndakupatsani leroŵa: kukonda Chauta, Mulungu wanu, ndi kumamtumikira ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse. Ndipo Iye azidzagwetsa mvula m'dziko mwanu pa nthaŵi yake, monga nthaŵi yadzinja ndiponso nthaŵi yachilimwe, kotero kuti mudzakhala ndi tirigu wambiri, vinyo wambiri ndiponso mafuta aolivi ambiri. Adzameretsa udzu woti ng'ombe zanu zizidzadya, ndipo inunso mudzapeza chakudya ndi kukhuta. Chenjerani, musasokeretsedwe ndi kutembenukira kwa milungu ina, kuti muziipembedza ndi kuitumikira, chifukwa Chauta adzakukwiyirani, adzakumanani mvula, ndipo nthaka sidzabalanso zipatso zake. Motero mudzaonongeka msanga m'dziko lokomali limene Chauta akukupatsani. Malamulo ameneŵa akhale m'mitima mwanu ndi m'maganizo mwanu. Muŵamange pamikono panu ndi pa mphumi pakati pa maso anu, kuti akhale chikumbutso. Muŵaphunzitse kwa ana anu. Muziphunzitsa mutakhala pansi m'nyumba mwanu, kapena muli paulendo, kapena mukupumula, kapena mukugwira ntchito. Alembeni pa mphuthu za zitseko za nyumba zanu ndi pa makomo anu. Pamenepo inu ndi ana anu, mudzakhala ndi moyo nthaŵi yaitali m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, adalumbira kuti adzapatsa makolo anu. Mudzakhala m'dziko limenelo nthaŵi zonse. Muzimvera mokhulupirika zonse zimene ndakuuzanizi. Muzikonda Chauta, Mulungu wanu, muzichita zonse zimene akulamulani, ndipo mukhale okhulupirika kwa Iye. Tsono pamene inu mukupita, Chauta adzapirikitsa mitundu ina yonseyo, ndipo mudzalanda maiko a mitundu ya anthu akuluakulu ndi amphamvu kupambana inu. Nthaka yonse imene mupondepoyo idzakhala yanu. Dziko lanulo lidzayambira ku chipululu kumwera, mpaka ku phiri la Lebanoni kumpoto, ndiponso kuyambira ku mtsinje wa Yufurate kuvuma, mpaka ku Nyanja Yaikulu kuzambwe. Palibe munthu ndi mmodzi yemwe amene adzakuletseni. Kulikonse kumene mudzapite m'dziko limenelo, anthu azidzakuwopani, monga momwe Mulungu wakulonjezerani kuti adzaŵachititsa mantha anthu amenewo. Lero ndikukupatsani zinthu ziŵiri kuti musankhepo, madalitso kapena matemberero. Madalitso kwa inu, mukamamvera malamulo a Chauta, Mulungu wanu, amene ndikukupatsani leroŵa. Koma matemberero kwa inu, mukapanda kumvera malamulo ameneŵa, nkusiya njira imene ndikukulamulani lero, kuti mutembenukire kwa milungu ina ndi kumaipembedza, milungu imene nkale lonse simudaipembedzepo. Chauta akadzakuloŵetsani m'dziko limene mukupita kukakhalamolo, muzikalalika madalitso ameneŵa mutakwera pa phiri la Gerizimu, koma matembereroŵa muzikaŵalalika mutakwera pa phiri la Ebala. Mapiri aŵiri ameneŵa ali chakuzambwe kutsidya kwa mtsinje wa Yordani, m'dziko la Akanani amene amakhala m'chigwa cha Yordani, pafupi ndi mitengo ya thundu ya ku More, kuyang'anana ndi Giligala. Muli pafupi kuwoloka Yordani ndi kukakhalamo m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsani. Mukakalilandira ndi kukhalamo, mukasamale kumvera malamulo ndi malangizo onse amene ndikukupatsani leroŵa. Naŵa malamulo ndi malangizo onse amene mudzayenera kuŵamvera nthaŵi zonse mudzakhale m'dziko limene Chauta, Mulungu wa makolo anu, akukupatsani. Mutalanda maiko a anthuwo, musadzalephere kuwononga kwathunthu malo onse amene iwo amapembedzerapo milungu yao, monga pa mapiri aatali ndi pa mapiri aafupi, ndiponso pansi pa mitengo yogudira. Mukagwetse maguwa ao, ndipo miyala yao yoimiritsa, imene amaiyesa yopembedzerapo, mukaiphwanyephwanye. Mukatenthe mafano ao a Aserimu. Mukaonongenso mafano ao ofanizira milungu yao, ndipo mukafafanize ndi dzina lomwe la milunguyo konsekonse. Musakapembedze Chauta, Mulungu wanu, monga m'mene amachitira anthu ameneŵa popembedza milungu yao. Mulungu adzasankha malo amodzi m'dziko mwanu, ndipo anthu onse azidzabwera kudzampembedza pa malo amenewo. Kumeneko ndiko kumene mudzapite. Muzikapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zanu zina, zopereka zanu zachikhumi, ndi zopereka za mtundu wina, ndiponso mphatso zimene mumalonjeza kupereka kwa Mulungu, zopereka zanu zaufulu, ndiponso ana oyamba kubadwa a ng'ombe ndi a zoŵeta zina. Kumenekonso inu pamodzi ndi mabanja anu mudzadya ndi kusangalala pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, chifukwa cha madalitso amene Iyeyo adatsitsa pa inu, kuti ntchito zanu zonse ziyende bwino. Nthaŵi imeneyo ikadzafika, musadzachite m'mene timachitira kunomu. Mpaka tsopano lino, aliyense mwa inu amangopembedza monga akufunira, poti simunaloŵebe m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsani ngati choloŵa chanu, kumene mudzatha kukhala mwamtendere. Mukaoloka mtsinje wa Yordani, Chauta, Mulungu wanu, adzakulolani kukakhala m'dziko limene Chauta adzakupatsani ngati choloŵa chanu. Adzakutchinjirizani kwa adani anu onse, kuti mukhale mwamtendere. Pamenepo Chauta adzasankhula malo oti anthu azidzapembedzerako, ndipo inu muzidzabwera kumeneko ndi zonse zimene ndakulamulanizi, monga nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zanu zinanso, zopereka zanu zachikhumi ndi zopereka zanu zina, ndiponso mphatso zanu zapadera zimene mumalonjeza kwa Chauta. Tsono mudzakondwa pamaso pake inuyo, ana anu aamuna ndi aakazi, antchito anu aamuna ndi aakazi, pamodzi ndi Alevi amene ali m'midzi mwanu, poti paja iwo sadzalandira dziko laolao. Musadzapereke nsembe zopsereza pamalo paliponse. Muzikapereka nsembezo pa malo amodzi okha, amene Chauta adzasankhule pakati pa mafuko anu. Muzikapereka nsembe zanu zopsereza pa malo okhawo, ndipo kumenekonso muzikachita zina zonse zimene ndikukulamulani. Ku midzi yonse kumene mukakhale, mungathe kumakaphako zoŵeta zanu kuti muzikadya. Muzidzadya monga mungafunire, malinga nchifundo cha Chauta, Mulungu wanu, chimene Iye wakupatsani. Nonsenu muzikadya, amene ali oipitsidwa pa zachipembedzo ndi amene ali osaipitsidwa. Monga momwe mukadadyera nyama yamphoyo kapena yangondo, muzikachita chimodzimodzi. Magazi okha a nyamazo musadzadye, koma muzikaŵataya pansi ngati madzi. Ku midzi yonse kumene mukakhale, musadzadye chachikhumi cha tirigu wanu, kapena cha vinyo wanu kapena cha mafuta anu aolivi. Kumenekonso musakadye kalikonse kamene mwakapereka kwa Chauta, monga ana a ng'ombe ndi a zoŵeta zina oyamba kubadwa, kapena mphatso zimene mwalonjeza kuti mudzapereka kwa Chauta, kapena zopereka zanu zaufulu, kapena zopereka zina zilizonse. Inuyo ndi ana anu, pamodzi ndi antchito anu, ndi Alevi amene akhala m'midzi mwanu, muzikadya zopereka zonsezi pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, pa malo amodzi amene Chauta, Mulungu wanu, adzakhala atasankha. Kumenekonso muzidzasangalala pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, chifukwa cha ntchito zanu zonse zoyenda bwino. Muchenjere kuti, nthaŵi zonse mudzakhale m'dzikomo, musadzaiŵale Alevi. Chauta, Mulungu wanu, akadzalikuza dziko lanulo monga momwe adakulonjezerani, pamene mudzamva nkhuli, mudzatha kukhuta nyama monga momwe mudzafunire. Ngati ali patali malo amene Chauta, Mulungu wanu, adasankha kuti anthu azilemekezerako dzina lake, mungathe kupha ng'ombe yanu iliyonse kapena choŵeta china, monga ndidakuuzirani. Muphe nyama mwa zimene Chauta akupatsani, ndipo mudye nyama kwanu, monga momwe mungafunire. Aliyense woipitsidwa pa zachipembedzo kapena wosaipitsidwa adyeko nyamayo, monga momwe akadadyera nyama yamphoyo kapena yangondo. Magazi okha musadye podya nyamayo, chifukwa moyo uli m'magazimo, motero inu musadye moyowo pamodzi ndi nyamayo. Magaziwo musadye, koma muŵataye pansi ngati madzi. Mukapanda kudya magaziwo, zonse zidzakuyenderani bwino inuyo ndi zidzukulu zanu, chifukwa cha kuchita zabwino motere pamaso pa Chauta. Zopereka zanu zimene mudapatulira Chauta pamodzi ndi mphatso zanu zimene mudalonjeza, zonsezo mupite nazo kwa Chauta pa malo achipembedzo amene adzaŵasankha. Kumeneko mukapereke nsembe zopsereza, nyama ndi magazi omwe, pa guwa la Chauta. Magazi ake mukathire pa guwa la Chauta, Mulungu wanu, koma nyama yake mungathe kudya. Musamale zonse zimene ndakulamulanizi, ndipo mumvere mokhulupirika. Muchite zabwino zokhazokha zokondweretsa Chauta, Mulungu wanu, kuti zonse zidzakuyendereni bwino, inu ndi zidzukulu zanu. Chauta, Mulungu wanu, akadzaononga mitundu ina imene mudzalanda dziko lao, inu mudzakhala ndi kukhazikika m'dzikomo. Chauta ataiwononga mitunduyo inu mukuwona, mukachenjere kuti musakatsate zipembedzo zao. Musadzayese kufunsafunsa za milungu yao kuti, “Kodi mitundu ya anthu iyi imapembedza bwanji milungu yao, kuti ifenso tichite chimodzimodzi?” Musadzapembedze Chauta, Mulungu wanu, mofanafana ndi m'mene iwo amapembedzera milungu yaoyo. Iwo adachita zoipa zoopsa zambiri zimene Chauta amadana nazo, mpaka kutentha ana ao aamuna ndi aakazi pa moto pakuŵapereka kwa milungu yao. Musamale bwino kuti muchite zonse zimene ndakulamulani. Musaonjezepo kapena kuchotsapo kanthu. Mwina mneneri kapena womasulira maloto adzaoneka pakati panupo, namanena kuti adzachita chizindikiro kapena chozizwitsa, Chizindikirocho kapena chozizwitsacho chikachitikadi, iye nakuuzani kuti mupembedze ndi kutumikira milungu ina imene simudaipembedzepo nkale lonse, inu musamvere zimenezo. Chauta, Mulungu wanu, akulola zimenezo kuti akuyeseni, kuti aone ngati mumamkondadi ndi mtima wanu wonse. Mutsate Chauta, Mulungu wanu, ndi kuwopa Iye yekha. Mutsate malamulo ake ndi kumvera mau ake. Mutumikire Iye ndi kuphathana naye. Koma aphedwe mneneri aliyense kapena womasulira maloto aliyense amene akuuzani kuti muukire Chauta, Mulungu wanu, amene adakutulutsani ku Ejipito ndi kukuwombolani m'dziko laukapolo. Munthu wotero ndi woipa, chifukwa akufuna kukusiyitsani njira imene Chauta akufuna kuti muitsate. Aphedwe, ndipo pakutero mudzachotsa choipa chimenechi pakati panu. Munthu atha kukunyengererani mobisa kuti mupembedze milungu ina, milungu imene inu ndi makolo anu simudaipembedzepo. Munthuyo ngakhale akhale mbale wanu weniweni wa mimba imodzi kapena mwana wanu wamwamuna kapena mwana wanu wamkazi, kapena mkazi wanu wokondedwa, kapena bwenzi lanu lapamtima, musaipembedze milunguyo mpang'ono pomwe. Milungu yake mwina idzakhala milungu ya anthu omwe mwayandikana nawo, kapena milungu ya amene mwatalikirana nawo. Inu musakopeke kapena kumvera zimene iyeyo akunena. Musamchitire chifundo kapena chisoni, ndipo musamtchinjirize. Mupheni! Yambani ndinu kumponya miyala, ndipo mutatero, pamenepo aliyense amponyenso miyala. Mumuphe ndi miyala. Iye adati akusokeretseni, kuti musiyane ndi Mulungu wanu amene adakutulutsani ku dziko la Ejipito kumene mudaali kuukapolo kuja. Tsono Aisraele onse adzamva zimene zachitikazo nadzachita mantha, ndipo palibe wina pakati panu amene adzachitenso choipa choterechi. Pomakhala m'midzi imene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsaniyo, nthaŵi zina kapena mudzamva kuti anthu ena a mtundu wanu asokeretsa anthu m'mizinda yao yomwe. Akuŵapembedzetsa milungu imene inu simudaipembedzepo nkale lonse. Mbiri yoteroyo muifufuze bwino. Mukapeza kuti mbiriyo njoona, kuti chinthu choipa choterechi chidachitikadi, pompo muphe anthu onse amumzindamo pamodzi ndi zoŵeta zomwe. Muwononge mudzi umenewo kotheratu. Zinthu zonse za anthu a mu mzinda umenewo muzisonkhanitse pamodzi, ndipo muziwunjike pakati pa bwalo lalikulu la mzindawo. Tsono mutatero, muutenthe mzindawo pamodzi ndi zonse zam'menemo, kuti zikhale ngati nsembe yopsereza kwa Chauta, Mulungu wanu. Muusiye choncho kuti ukhale bwinja mpaka muyaya. Musagwireko kanthu kena kalikonse koyenera kuwonongedwa. Tsono Chauta adzaleka osakukwiyiraninso, adzakumverani chisoni ndipo adzakuchitirani chifundo, nadzakuchulukitsani monga adalonjezera makolo anu. Adzakuchitirani zimenezi mukamamvera mau a Chauta, Mulungu wanu, mukamatsata malamulo ake amene ndikukuuzani lero, ndipo mukamachita zolungama pamaso pa Chauta, Mulungu wanu. Inu ndinu anthu a Chauta, Mulungu wanu. Mukamalira maliro, musamadzichekacheka kapena kudzimeta pamphumi. Ndinu ake a Chauta, Mulungu wanu, popeza kuti wakusankhulani pakati pa anthu a pa dziko lonse lapansi, kuti mukhale anthu akeake. Chilichonse chimene Chauta akuti nchonyansa, musadye. Nyama zoti muzidya ndi izi: ng'ombe, nkhosa, mbuzi, ngondo, nswala, mphoyo, mphalapala, ngoma, nyumbu ndi mbalale. Mungathe kudya nyama iliyonse imene ili ndi ziboda zogaŵikana ndiponso yobzikula. Koma pakati pa nyama zaziboda kapena zobzikula, musadye izi: ngamira, kalulu ndi mbira, chifukwa ngakhale zimabzikula, koma zilibe ziboda zogaŵikana. Nkhumbanso ndi yonyansa kwa inu. Ziboda ili nazo, komatu sibzikula. Nyama zimenezi musamadya, ndipo musamazikhudza zikafa. Mwa zonse zokhala m'madzi mungathe kudya izi: zonse zimene zili ndi zipsepse ndi mamba. Koma zonse zopanda zipsepse ndi mamba ndi zonyansa kwa inu, choncho musadye. Mbalame zonse zoyenera kuzidya, mudye. Koma mbalame zosayenera kuzidya ndi izi: mphungu, nkhwazi, mwimba, kamtema, khungubwi ndi mtundu uliwonse wa mwimba, mtundu uliwonse wa akhungubwi, nthiŵatiŵa, chipudo, kakoŵa, mtundu uliwonse wa akabaŵi, nkhutukutu, mantchichi, tsakwe, vuwo, dembo, chiswankhono, indwa ndi chimeza ndi zina za mtundu umenewu, ndiponso nsadzu ndi mleme. Ziwala zonse zamapiko ndi zonyansa, choncho musadye zimenezo. Koma zonse zamapiko zosaipitsidwa mungathe kudya. Nyama iliyonse yofa yokha, musadye. Alendo okha amene mumakhala nawo, alekeni adye, kapena mungogulitsa nyamayo kwa alendo ena. Pajatu inu ndinu opatulika a Chauta, Mulungu wanu. Musaphike mwanawankhosa kapena mwanawambuzi mu mkaka wa make. Chachikhumi muziika padera, ndiye kuti limodzi mwa magawo khumi a zokolola zanu za chaka ndi chaka. Tsono pitani mukakhale pa malo amodzi amene Chauta, Mulungu wanu, adzasankhula kuti anthu azidzampembedzerapo. Ndipo magawo achachikhumi ameneŵa mudyere pa malo amenewo, pamaso pa Mulungu wanu. Magawo ameneŵa ndi a tirigu, vinyo ndi mafuta aolivi, ndiponso ana oyamba kubadwa a ng'ombe ndi a nkhosa. Muzichita zimenezi masiku onse, kuti motero muphunzire kuwopa Chauta, Mulungu wanu. Koma mwina mtunda udzakutalikirani chifukwa kwatalikitsa kumalo kumene Chauta, Mulungu wanu, adasankhula kuti anthu azimpembedzerako. Motero inu mudzalephera kupita nawo kumeneko magawo anu achachikhumiwo, amene mwaŵapeza chifukwa cha madalitso a Chauta, Mulungu wanu. Pamenepo mugulitse zinthuzo, ndipo ndalama zake mupite nazo ku malo achipembedzowo. Ndalamazo mugulire zilizonse zimene mufuna, monga nyama yang'ombe, nyama yankhosa, vinyo ndiponso zakumwa zaukali, malinga nkukhosi kwanu. Tsono inuyo pamodzi ndi mabanja anu, mudzadye ndi kusangalala pamaso pa Chauta, Mulungu wanu. Koma Alevi amene mumakhala nawo m'midzi mwanu musaŵaiwale, popeza kuti alibe dziko kapena choloŵa chaochao. Chaka chachitatu chilichonse muzibwera ndi magawo onse achachikhumi ochokera ku zopereka zanu za chaka chimenecho, ndi kuŵaika poyera m'midzi mwanu. Chakudya chimenechi ncha Alevi, poti alibe zaozao. Ndiponso ncha alendo ndi cha ana amasiye ndi akazi amasiye amene amakhala nanu pamodzi m'midzi mwanu. Anthu otere azibwera kudzatenga zimene akusoŵa. Muzichita zimenezi kuti Chauta, Mulungu wanu, adzakudalitseni pa ntchito zanu zonse. Chikatha chaka chachisanu ndi chiŵiri chilichonse, muzikhululukira onse amene adakongola zinthu zanu. Zimenezi zizichitika motere: aliyense amene adakongoza Mwisraele mnzake ndalama, afafanize ngongole imeneyo. Asamuumirize kapena mbale wake kuti abweze ndalamazo, popeza kuti Chauta walamula kuti ngongoleyo ifafanizidwe. Mungathe kulonjerera ngongole kwa mlendo yekha, koma ngongole ya munthu wa mtundu wanu muifafanize. Palibe ndi mmodzi yemwe mwa anthu a mtundu wanu amene adzasauke, (poti Chauta, Mulungu wanu, adzakudalitsani m'dziko limene Iye adzakupatsani ngati choloŵa chanu,) malinga mukamamvera mau ake ndi kusamala zotsata malamulo amene ndikukulamulani leroŵa. Chauta adzakudalitsani inu monga momwe adalonjezera. Mudzakongoza mitundu yambiri, koma inuyo simudzakongola kwa wina aliyense. Mudzalamulira mitundu yambiri, koma palibe mtundu wina uliwonse umene udzakulamulireni inu. Pakati pa abale anu pakakhala wina wosauka m'midzi yanu, m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo, musadzaume mtima, ndipo musadzaume manja. Makamaka muzidzamchitira chifundo ndi kumkongoza monga momwe angafunire. Musadzakhale ndi maganizo achabe akuti, “Chaka chofafaniza ngongole chili pafupi.” Mukapanda kumuwonetsa mtima wachifundo mbale wanu wosaukayo, osampatsa kanthu, iyeyo adzakunenezani kwa Chauta molira, ndipo mudzapezeka olakwa. Dzampatseni mwaufulu mosaŵinya, ndipo Chauta adzakudalitsani pa ntchito zanu zonse. Nthaŵi zonse padzakhala Aisraele ena osauka, osoŵa zinthu. Motero ndikukulamulani kuti otereŵa muzidzaŵachitira chifundo. Muhebri mnzanu, mwamuna kapena mkazi, akadzigulitsa kwa inu kuti akhale kapolo wanu, mummasule atangokutumikirani zaka zisanu ndi chimodzi zokha. Pa chaka chachisanu ndi chiŵiri, mumlole kuti apite mwaufulu. Mukammasula, musangomchotsa ali chimanjamanja. Mpatseniko momkomera mtima zonse zimene Chauta adakudalitsa nazoni monga: nkhosa, tirigu ndi vinyo. Kumbukirani kuti mudaali akapolo ku Ejipito, ndipo Chauta, Mulungu wanu, adakuwombolani. Nchifukwa chake ndikukupatsani lamulo limeneli tsopano lino. Koma kapoloyo akakhala kuti akukukondani inu ndi banja lanu, chifukwa mukukhala naye bwino, mwina sangafune nkuchoka komwe. Ngati zili choncho, mutenge zingano ndipo muboole khutu la kapoloyo, mpaka zinganoyo iloŵe m'chitseko. Mukatero, adzakhala kapolo wanu moyo wake wonse. Ngati ndi kapolo wamkazi, mudzamchite chimodzimodzi. Kumasula kapolo, kuti akhale mfulu, kusakuipireni. Adakutumikirani kale zaka zisanu ndi chimodzi pa theka la mtengo wa wantchito wolembedwa. Chitani zimenezi, ndipo Chauta, Mulungu wanu, adzakudalitsani pa ntchito zanu zonse. Ana onse amphongo oyamba kubadwa a ng'ombe ndi a zoŵeta zina, muŵapatule kuti akhale a Chauta, Mulungu wanu. Ng'ombe zimenezi musazigwiritse ntchito, ndipo nkhosazo musazimete bweya. Chaka ndi chaka inu, pamodzi ndi banja lanu, muzidya zimenezi pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, ndiponso ku malo amene Chauta adzasankhe. Koma ngati pali kanthu kolakwika pa nyamayo, monga kutsimphina kapena khungu, kapena chilema chilichonse, musaphere nsembe Chauta nyama yoteroyo. Nyama zotero, mudyere kwanu. Nonsenu, kaya ndinu oyeretsedwa pa za chipembedzo kapena ai, mungathe kudya zimenezo, monga momwe mumadyera mphoyo kapena ngondo. Magazi okha musadye, koma mungoŵataya pansi ngati madzi. Muzilemekeza Chauta, Mulungu wanu, pakuchita chikondwerero cha Paska pa mwezi wa Abibu. Chifukwa usiku wina mwezi umenewu, mpamene Chauta adakutulutsani ku Ejipito. Muzipereka nsembe za chikondwerero cha Paska kwa Chauta, Mulungu wanu. Muphe nkhosa kapena ng'ombe pa malo amene Chauta adzasankhule kuti anthu azidzapembedzerapo. Nyama ya nsembeyo musadye ndi buledi wotupitsa. Pa masiku asanu ndi aŵiri, muzidya nyamayo ndi buledi wosatupitsa ndiye kuti buledi wamazunzo, pakuti mudatuluka ku Ejipito mothaŵa. Motero masiku onse a moyo wanu, mudzakumbukira tsiku limene mudatuluka ku Ejipito. Pa masiku asanu ndi aŵiri munthu wina aliyense asadzasunge chofufumitsira buledi m'nyumba mwake m'dziko mwanumo. Nyama imene idaphedwa madzulo pa tsiku loyamba, muzidzaidya kusanache. Musapereke nsembe ya Paska kulikonse ku dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsani. Muziphera pa malo amodzi opembedzerapo aja. Muzichita zimenezi poloŵa dzuŵa, ndiye kuti nthaŵi yomwe ija imene mudachoka ku Ejipito. Muziphika nyamayo ndi kuidyera pa malo achipembedzo amodziwo, ndipo muzibwerera ku zithando zanu m'maŵa mwake. Masiku asanu ndi limodzi muzidya buledi wosatupitsa. Koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, muzisonkhana kuti mupembedze Chauta, Mulungu wanu, ndipo musadzagwire ntchito pa tsiku limenelo. Muŵerenge masabata asanu ndi aŵiri kuyambira nthaŵi imene mwayamba kudula tirigu. Tsono muchite chikondwerero cha kholola, cholemekeza Chauta, Mulungu wanu, pakumpatsa chopereka chaufulu, molingana ndi madalitso amene Iye wakupatsani. Mukhale okondwa pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, inuyo pamodzi ndi mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, mtumiki wamu wamwamuna, mdzakazi wanu, Alevi amene ali m'mizinda mwanu, alendo, ana amasiye ndi akazi amasiye, amene amakhala nanu pamodzi m'mizinda mwanu. Zimenezi muzichitira pa malo opembedzerapo aja. Kumbukirani kuti mudaali akapolo ku Ejipito. Motero malamulo ameneŵa muziŵasungadi mosamala. Mutatuta tirigu wanu yense, ndiponso mutafinya mphesa zanu, muzidzachita chikondwerero cha misasa masiku asanu ndi aŵiri. Musangalale pa chikondwererocho, inuyo pamodzi ndi mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, mtumiki wanu wamwamuna, mdzakazi wanu, Alevi amene ali m'mizinda mwanu, alendo, ana amasiye ndi akazi amasiye, amene amakhala nanu m'mizinda mwanu. Muzidzatamanda Chauta, Mulungu wanu, pochita chikondwerero chimenechi masiku asanu ndi aŵiri, pa malo amene Iye adzasankhule, chifukwa chakuti Chauta, Mulungu wanu, adzakhala atadalitsa kholola lanu ndi ntchito zanu zonse, kuti chimwemwe chanu chikhale chodzaza ndithu. Anthu aamuna onse a mtundu wanu azidzabwera kudzapembedza Chauta, Mulungu wanu, ku malo achipembedzo, katatu pa chaka. Azidzafika pa nthaŵi ya Paska, pa nthaŵi ya chikondwerero cha kholola ndiponso pa nthaŵi ya chikondwerero cha misasa. Ndipo pobwera pamaso pa Chauta, asamadzakhale chimanjamanja, koma munthu aliyense azidzabwera ndi mphatso monga momwe angathere, molingana ndi madalitso amene Chauta, Mulungu wanu, adampatsa. M'fuko lililonse mudzasankhe anthu oweruza ndiponso akuluakulu ena mu mzinda uliwonse umene Chauta, Mulungu wanu, adzakupatseni. Anthu ameneŵa azidzaweruza anzao mosakondera. Asadzachite zinthu mopanda chilungamo kapena kuweruza milandu mokondera. Asadzalandire chiphuphu, chifukwa ziphuphu zimadetsa m'maso ngakhale anthu anzeru ndipo zimalakwitsa anthu olungama poweruza. Mukonde osati china ai, koma chilungamo chokha basi, kuti mudzalandiredi dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsani ngati choloŵa chanu, ndi kukhazikikamo. Musadzazike mtengo uliwonse wachipembedzo pambali pa guwa la Chauta, Mulungu wanu, limene mudzamange. Ndipo musadzaimiritse miyala yachipembedzo, popeza kuti Chauta, Mulungu wanu, amadana nazo zimenezi. Musadzapereke ng'ombe kapena nkhosa yachilema ngati nsembe kwa Chauta, Mulungu wanu. Musadzapereke nyama iliyonse yopunduka, chifukwa Mulungu wanu amadana nazo zimenezi. Mwina padzapezeka kuti mu mzinda wina umene Chauta, Mulungu wanu, wakupatsani, muli munthu wina wamwamuna kapena wamkazi amene wachimwira Chauta, Mulungu wanu, naphwanya chipangano chake, popembedza ndi kutumikira milungu ina, monga dzuŵa, mwezi kapena nyenyezi, zimene ndidaletsa kuti asazipembedze. Mukamva kuti chinthu chotere chachitika, mufufuze bwino nkhani imeneyo, ndipo mukapeza kuti choipa choterechi chachitikadi mu Israele, mumgwire mwamunayo kapena mkaziyo ndi kupita naye ku zipata za mzinda wanu ndipo mumphere kunja kwa mzinda pakumponya miyala. Munthuyo aphedwe pokhapokha patapezeka mboni ziŵiri kapena zitatu. Asaphedwe chifukwa cha umboni wa munthu mmodzi yekha. Ziyambe ndi mbonizo kuponya miyala. Pambuyo pake anthu onse amponye miyala munthuyo. Motero chinthu choipacho mudzachichotsa pakati panu. Milandu yophana, yolimbirana zinthu, kapena yopwetekana m'mizinda mwanu, ikaŵavuta aweruzi anu, mupite ku malo achipembedzo aja osankhidwa ndi Chauta, Mulungu wanu, ndipo mupereke mlandu wanuwo kwa ansembe Achilevi ndi kwa muweruzi amene ali pa ntchito pa nthaŵi imeneyo. Ndipo iwowo agamule mlanduwo. Iwowo atagamula, inu muyenera kungochita zomwe akuuzani ku malo osankhidwa ndi Chauta. Muvomere chiweruzo chao, ndipo mutsate malangizo ao onse, osapotokera kumanja kapena kumanzere. Aliyense wosamvera wansembe amene akutumikira Chauta, Mulungu wanu, kapena wosamvera muweruzi, aphedwe. Mwa njira imeneyi mudzachotsa choipa pakati pa Aisraele. Tsono aliyense amene adzamve zimenezi adzakhala ndi mantha, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adzafune kuchitanso zotere. Mutaloŵa ndi kukhazikika m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, adzakupatsenilo, ndipo mukadzafuna kuti mukhale ndi mfumu monga ili nayo mitundu ina yozungulira, mfumu imeneyo idzakhale munthu wosankhidwa ndi Chauta, Mulungu wanu. Adzakhale munthu wa mtundu wanu. Musadzasankhe mlendo kuti akhale mfumu yanu, ameneyo si mbale wanu. Mfumuyo isadzakhale ndi akavalo ambiri ndipo isadzatume anthu ku Ejipito kukagula akavalo, popeza kuti Chauta adakuuzani kuti, “Musadzabwererenso kumeneko.” Mfumu isadzakhale ndi akazi ambiri kuti mtima wake ungadzapotoke. Ndipo isadzadzikundikire siliva ndi golide wambiri. Munthuyo ataloŵa mu ufumu wakewo, adzalembe m'buku lakelake malamulo a Mulunguŵa ochokera mu buku la malamulo limene lili m'manja mwa ansembe Achilevi. Buku limeneli adzalisunge ndipo azidzaŵerengamo pa moyo wake wonse, kuti adzaphunzire kuwopa Chauta, Mulungu wake, pakutsata mokhulupirika zonse zolembedwa m'bukumo. Zimenezi zidzamthandiza kudziŵa kuti iyeyo saposa Aisraele anzake, ndiponso kuti sayenera kukhala wonyozera malamulo a Chauta mpang'ono pomwe. Motero iyeyo, pamodzi ndi zidzukulu zake zomwe, adzalamulira nthaŵi yaitali mu Israele. Ansembe Achilevi, ndiye kuti fuko lonse la Alevi, asalandireko gawo m'dziko la Israele ngati choloŵa chao. Iwoŵa azidya zoperekedwa nsembe kwa Chauta ndi zina zoyenera Iyeyo. Asakhale ndi choloŵa ngati mafuko ena. Choloŵa chao ndi Chauta amene, potsata malonjezo a Mulungu yemweyo. Mwa zopereka za anthu, zoyenera kuzilandira ansembeŵa, ndi izi: ng'ombe kapena nkhosa zodzaperekera nsembe, mwendo wamwamba, nyama yam'chibwano ndi chifu. Ansembe azilandiranso gawo lanu loyambayamba la tirigu, la vinyo, la mafuta aolivi ndiponso la ubweya. Pa mafuko anu onseŵa Chauta adasankhulapo anthu a fuko la Levi ndi ana ao, kuti azigwira ntchito zaunsembe nthaŵi zonse. Mlevi aliyense atafuna, angathe kubwera ku malo osankhidwa ndi Chauta kuchokera m'mudzi wina uliwonse ku Israele kumene akukhala. Ndipo kumeneko atumikire Chauta, Mulungu wake, pa unsembe, monga momwe achitira Alevi ena onse amene akutumikira kumeneko. Ayenera kulandira chakudya molingana ndi ansembe ena, ngakhale ali ndi ndalama chifukwa chogulitsa za m'banja mwake. Mukadzaloŵa m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo, musakatsate machitidwe onyansa a mitundu ya anthu akumeneko. Pakati panu pasadzapezeke wopereka mwana wake wamwamuna kapena wamkazi pa moto ngati nsembe. Pasaoneke munthu woombeza kapena woyeseza kulosa zam'tsogolo, kapena wogwiritsa ntchito nyanga kapena zithumwa. Pasapezekenso munthu wopempha nzeru kwa mizimu ya anthu akufa. Chauta, Mulungu wanu, amadana nawo anthu ochita zoipa zimenezi. Chimene Mulungu akupirikitsira anthuŵa pamene inu mukufika ndi chifukwa chakuti anthuwo ankachita zoipa zoterezi. Inu mukhale okhulupirika kwathunthu kwa Chauta, Mulungu wanu. Anthu amene mukukaŵalanda dziko limene mukakhalemolo, amatsata ndi kumvera amatsenga ndi oombeza. Koma inuyo Chauta, Mulungu wanu, sakulolani kuchita zimenezi. Iye adzakutumizirani mneneri wonga ine wochokera mwa inu amene, ndipo mudzayenera kumumvera iyeyo. Pa tsiku lija mudaasonkhana pa phiri la Horebuli, mudaapempha kuti, “Tisamvenso Chauta, Mulungu wathu, akulankhula, ngakhale kuwonanso moto waukulu choterewu, kuti tingafe.” Apo Chauta adaandiwuza kuti, “Zonse zimene apemphazi anena mwanzeru. Ndidzaŵatumizira mneneri wonga iwe, wochokera mwa iwo amene. Ndidzamuuza zoti anene, ndipo iyeyo azidzauza anthu zonse zimene ndikumlamula. Mneneriyo akalankhula m'dzina langa, Ine ndidzalanga aliyense wosamvera mau angawo. Koma mneneri wina aliyense woyerekeza kulankhula m'dzina langa, Ine osamulamula kuti atero, aphedwe. Ndipo ayeneranso kuphedwa mneneri wina aliyense wolankhula m'dzina la milungu ina.” Mwina mwake munganene kuti, “Kodi munthu angadziŵe bwanji kuti mau a mneneri wakutiwakuti sakuchokera kwa Chauta?” Munthu akati akulankhula m'dzina la Chauta, ndipo ngati zolankhula zakezo sizichitika, pomwepo dziŵani kuti si mau a Chauta amenewo. Mneneri ameneyo wongolankhula zakezake modzikhulupirira, musamuwope ai. Chauta, Mulungu wanu, ataononga eniake a dziko limene akukupatsanilo, ndipo inu mutalanda mizinda yao pamodzi ndi nyumba zao, nkukhazikika kumeneko, mudzapatule mizinda itatu m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, adzakupatsenilo. Mudzakonze miseu yake, ndipo mudzaligaŵe patatu dzikolo. Choncho kudzakhala malo amene munthu wopha mnzake adzatha kuthaŵirako. Nali lamulo lokhalira munthu wopha mnzake, amene angapulumutse moyo wake pothaŵira kumeneko: Munthu akapha mnzake mwangozi, osati chifukwa cha chidani, athaŵire ku mzinda uliwonse mwa mizinda imeneyo kuti apulumuke. Mwachitsanzo, anthu aŵiri apita ku thengo limodzi kukadula mitengo. Wina podula mtengo, nkhwangwa nkuguluka, nipha mnzakeyo. Iye angathe kuthaŵira ku umodzi mwa mizinda imeneyi, napulumuka. Akapanda kutero, mwina chifukwa cha kutalika kwa mtunda, wachibale wofuna kumlipsira adzamthamangira mwaukali, nkumugwira wothaŵayo namupha, ngakhale ali wosayenera kuphedwa, chifukwa paja popha munthu mwangozi analibe chidani chilichonse ndi amene adafayo. Nchifukwa chake ndikukulamulani kuti mupatule mizinda itatu. Chauta, Mulungu wanu, akadzakuza dziko lanu monga momwe adalonjezera makolo anu, ndipo akadzakupatsani dziko lonse limene adalonjeza, pamenepo mudzapatulenso mizinda ina itatu. Adzakuwonjezerani dziko ndithu, malinga mukamakachita zonse zimene ndikukulamulani, ndiye kuti kukonda Chauta, Mulungu wanu, ndi kuchita zonse zimene akukuphunzitsani. Muzidzachita zimenezi kuti musadzalakwe pakupha anthu osachimwa m'dziko limene Chauta akukupatsanilo. Mwina mwake munthu adana ndi mnzake, ndipo amkhalizira namupha mwadala, nkuthaŵira ku umodzi mwa mizinda imeneyi kuti apulumuke. Zikatero, akuluakulu akwao adzamuitanitse kuchokera ku mzinda wakewo, ndi kukampereka kwa woyenera kumlipsira uja kuti aphedwe ndithu. Musamchitire chifundo. Mchotseni pakati pa Aisraele munthu wopha mnzake wosalakwa, kuti zinthu zikuyendereni bwino. M'choloŵa chomwe mudzakhala mutalandira m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo, musakaŵafutuze malire a mnzanu amene anthu akale adakhazika. Mboni imodzi sikwanira kumtsimikiza munthu kuti wachimwadi kapena kuti wapalamuladi mlandu pakuchita cholakwa chakutichakuti. Chofunika nchakuti pakhale mboni ziŵiri kapena zitatu zotsimikiza kuti munthuyo walakwadi. Munthu wina akaneneza mnzake momnamizira kuti walakwa, aŵiri onsewo abwere, adzaimirire pamaso pa Chauta. Kumeneko aŵaweruze ansembe ndi aweruzi amene ali pa ntchito nthaŵi imeneyo. Aweruziwo adzafufuze za mlanduwo. Akapeza kuti munthu uja ndi mboni yachabe ndipo kuti waneneza mnzake monama, amlange pomchita choipa chimene iyeyo anati achite mnzake. Mwa njira imeneyi, mudzachotsa choipa chimenechi pakati pa inu. Tsono wina aliyense akadzamva zimene zachitika, adzakhala ndi mantha, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe mwa inu amene adzachitenso choipa choterechi. Musachite chifundo. Chilango chake chikhale chakuti moyo ulipe moyo, diso lilipe diso, dzino lilipe dzino, dzanja lilipe dzanja, ndipo phazi lilipe phazi. Mukadzapita kukamenyana ndi adani anu, ngati muwona kuti magaleta ao ngochuluka kuposa anu, ngamira zao ndi zochulukanso, ndipo ngakhale ankhondo ao omwe ngokuposani, musakaŵaope. Chauta, Mulungu wanu, amene adakupulumutsani ku Ejipito, adzakhala nanu. Musanayambe kumenya nkhondo, wansembe abwere, ndipo auze ankhondowo kuti, “Imvani, inu Aisraele! Lero mukuyamba kumenya nkhondo ndi adani anu. Musataye mtima ai! Musaŵaope adaniwo, musanjenjemere, musachite mantha. Chauta, Mulungu wanu, apita nanu Iye yemwe kuti akuthandizeni pa nkhondoyo ndipo kuti akupambanitseni.” Pamenepo akuluakulu a ankhondo adzauza anthu kuti, “Kodi alipo pano munthu amene wangomanga nyumba yatsopano, koma sanaipereke kwa Mulungu? Ngati alipo abwerere kwao, mwinamwina akaphedwa pa nkhondo, ndiye kuti ndi wina amene adzaipereka nyumbayo. Kodi alipo pano wina amene wangooka mipesa m'munda, koma osakhala ndi mwai woti nkuthyola mphesa zake? Ngati alipo abwerere kwao, mwinamwina akaphedwa pa nkhondo, ndiye kuti ndi wina amene adzamwe vinyoyo. Kodi alipo wina pano amene adafunsira mbeta koma mkaziyo sanaloŵane naye? Ngati alipo, abwerere kwao, mwinamwina akaphedwa pa nkhondo, ndiye kuti ndi wina amene adzakwatire mbetayo.” Pamenepo akuluakuluwo adzafunsanso anthu kuti, “Kodi alipo pano wina aliyense amene akuwopa ndipo mtima wake wafumuka ndi mantha? Ngati alipo, abwerere kwao, kuti angamakadederetse anzake.” Akuluakulu atamaliza kulankhula ndi gulu lankhondolo, asankhe mtsogoleri pa gulu lililonse. Mukamapita kukathira nkhondo mzinda, poyamba apatseni anthu amumzindawo mwai woti agonje okha. Akakutsekulirani zipata nakugonjerani, akhale akapolo anu onsewo, ndipo akugwirireni ntchito yaukapolo. Koma ngati anthu a mu mzinda umenewo akana kugonja, nasankhula nkhondo, uzingeni mzindawo ndi gulu lanu lankhondo. Chauta, Mulungu wanu, akakulolani kugonjetsa mzindawo, muphe mwamuna aliyense m'menemo. Koma akazi ndi ana mungoŵagwira, ndipo mutengenso zoŵeta ndi zonse zimene zili mumzindamo ngati zofunkha zanu. Zinthu zonse za adani anu muzigwiritse ntchito, Chauta wakupatsani zimenezo. Umu ndi m'mene muzikachitira ndi mizinda ya kutali ndi inu, imene siili mizinda ya anthu akuno. Koma mukadzalanda mizinda imene ili m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsaniyo, muphe aliyense. Muŵaononge kotheratu onse anthu aŵa: Ahiti, Aamori, Akanani, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi, monga momwe Chauta Mulungu wanu adakulamulirani. Iphani onse, kuti angadzakuchimwitseni kuchimwira Chauta, Mulungu wanu, pokuphunzitsani zoipa zimene iwowo amachita akamapembedza milungu yao. Pamene muzinga mzinda nthaŵi yaitali ndi cholinga choti muulande, musagwetse mitengo yake yazipatso, mungathe kudya zipatso zake, koma mitengo yake musagwetse, chifukwa adani anu si mitengoyo. Koma mitengo ina yosabereka zipatso mungathe kuidula ndi kumagwira nayo ntchito popanga makina ankhondo okhalirira mzinda umene mukulimbana nawo mpaka mutaugonjetsa. M'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsani kuti likhale lanulanu mwina mwake mungathe kupeza munthu wakufa m'munda, inu osadziŵa amene wamupha. Akuluakulu anu ndi aweruzi anu apiteko, ndipo akayese kutalika kwake kuchokera pamalo pamene pali munthu wakufayo mpaka ku mizinda yoyandikana ndi malowo. Pamenepo akuluakulu a mudzi woyandikana kwambiri ndi pamene pali mtembopo, asankhe ng'ombe imene sidagwirepo ntchito, ndipo sidakokepo galeta. Ng'ombeyo apite nayo kudambo kumene kuli madzi oyenda. Malowo akhale akuti munthu sadalimepo nkale lonse kapena kubzalapo kanthu. Kumeneko akaithyole khosi ng'ombeyo. Ansembe Achilevi apitekonso kumeneko, chifukwa ndiwo amene ayenera kumaweruza milandu yonse ya ndeu ndi ya kupha. Chauta, Mulungu wanu, wasankha iwowo kuti akhale atumiki ake, ndiponso kuti azidalitsa m'dzina lake. Tsono atsogoleri onse ochokera ku mudzi wa pafupi ndi pamene panali munthu wophedwayo, asambe m'manja pamwamba pa ng'ombe ija imene adaithyola khosi m'dambo muja. Ndipo anene kuti, “Sindife tidamupha munthuyu, ndipo amene adamupha sitidamuwone. Inu Chauta, khululukirani anthu anu Aisraele amene mudaŵaombola. Tikhululukireni ndipo musaike pa ife tchimo la kupha munthu wosalakwayu.” Mukachita zimene Chauta afuna, Iyeyo sadzakuzengani mlandu woti mwapha munthu wosalakwa. Chauta, Mulungu wanu, akakupambanitsani pa nkhondo, mungathe kugwirapo akapolo kunkhondoko. Mwina pakati pa akapolowo inu nkuwona mkazi wokongola amene mwamkonda, ndipo mufuna kumkwatira. Pita nayeni kwanu, ndipo mkaziyo amete kumutu, ndi kutseteka makadabo ake, ndipo asinthe zovala. Akhale m'mudzi mwanu mwezi wathunthu, ndipo alire maliro kulira makolo ake. Tsono atatha zimenezi, mumkwatire. Pambuyo pake mutaona kuti simukumfunanso, mumleke, apite mwaufulu kumene akufuna. Simungathe kumuyesanso kapolo kapena kumgulitsa, chifukwa mudakhala naye malo amodzi. Tiyese kuti munthu ali ndi akazi aŵiri, wina wokondedwa kwambiri wina pang'ono, onsewo nkubala ana aamuna, mwana woyamba kubadwa nakhala wa mkazi amene amamkonda pang'ono. Munthuyo akatsimikiza zoti agaŵire ana akewo chuma chake, asakondere mwana wa mkazi wokondedwa koposayo, pakumpatsa gawo la mwana woyamba. Mwana wake woyamba kubadwa uja ampatse moŵirikiza, ngakhale kuti ndi mwana amene mai wake ndi wokondedwa pang'ono. Munthu ayenera kuvomera mwana wake woyamba, ndi kumpatsa gawo limene lili lake potsata lamulo. Tiyese kuti wina ali ndi mwana wokanika ndiponso wachipongwe, mwana woti bambo ndi mai ake saŵamvera konse, ngakhale amlange chotani. Makolo ake a mwanayo amgwire ndi kupita naye kwa akuluakulu amumzinda ku chipata cha mzindawo. Makolowo auze akuluakuluwo kuti, “Mwana wathu ndi wokanika ndipo ndi wachipongwe safuna kutimvera, ndi wadyera ndiponso chidakwa. Pamenepo anthu amumzindawo amuphe pakumponya miyala, motero mudzachotsa choipa pakati panu. Anthu onse a mu Israele muno akadzamva zimene zachitikazi, adzakhala ndi mantha.” Munthu akaphedwa chifukwa cha mlandu, ndipo mtembo wake ndi wopachikidwa pa mtengo, mtembowo usagonere pamtengopo. Uikidwe tsiku lomwelo, chifukwa kuti mtembo ugonerere pamtengo ndi chinthu chobweretsa matemberero a Mulungu. Kwirirani mtembowo, kuwopa kuti mungaipitse dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo. Mukaona ng'ombe kapena nkhosa ya Mwisraele mnzanu ikusokera, musailekerere. Itengeni, mukampatse mwiniwake. Koma ngati mwiniwake kwao nkutali, kapena simumdziŵa, itengeni mupite nayo kwanu, muisunge komweko. Koma mwiniwake akabwera kudzaifunafuna, mumpatse. Mukapeza bulu, chovala kapena kanthu kena kalikonse kamene Mwisraele mnzanu wataya, chitani chimodzimodzi, musakalekerere ai. Bulu wa Mwisraele mnzanu akagona mu mseu, muutseni. Muchitenso chimodzimodzi ndi ng'ombe yake, musailekerere. Mthandizeni mnzanu kuti adzutse choŵetacho. Akazi asamavale zovala za amuna, chimodzimodzi amuna asamavale zovala za akazi. Chauta, Mulungu wanu, amanyansidwa nawo anthu ochita zotere. Ngati mupeza chisa cha mbalame mu mtengo kapena pansi, make ali pa mazira, kapena ali ndi tiana take, musaitenge mbalameyo pamodzi ndi tiana take. Tianato mungathe kutenga, koma makeyo mloleni apite, kuti mukakhale ndi moyo wabwino ndi wautali. Pamene mukumanga nyumba, muwonedi kuti mwamanga kampanda pamwamba kuzungulira mbali zonse zadenga. Apo inuyo simudzazengedwa mlandu wa kukhetsa magazi ngati wina agwa kuchokera pa denga, naphedwa. M'munda wamphesa musabzalemo mbeu ina iliyonse. Ngati mutero, zonse zidzakhala zoletsedwa, mphesazo ndi mbeu zina zomwe. Musamange ng'ombe ndi bulu kuti zilimire pamodzi. Musamavale nsalu yoombedwa ndi ubweya pamodzi ndi thonje. Sokani mphonje pa ngodya zinai za miinjiro yanu imene mumavala. Mwina munthu angathe kukwatira mtsikana, namakhala naye ndithu, pambuyo pake nkunena kuti mkaziyo sakumfuna. Tsono ayamba kumnenera zabodza zochititsa manyazi ndi kuipitsa mbiri yake ponena kuti, “Mkazi ameneyu sadaoneke ngati namwali wosadziŵa mwamuna pa nthaŵi yomukwatira.” Zitatero, makolo a mkaziyo atenge zizindikiro zotsimikizira akuluakulu abwalo am'mudzimo kuti mwana waoyo adaali namwali wosadziŵa mwamuna ndithu. Pamenepo bambo wake wa mtsikanayo aŵauze abwalowo kuti, “Ndidalola mwana wanga wamkazi kuti akwatiwe ndi munthu uyu, koma tsopano akuti sakumufuna. Wamnamizira momchititsa manyazi kuti ati sadali namwali wosadziŵa mwamuna pomkwatira. Koma pano tili ndi umboni wotsimikizira kuti mwana wangayu adaali namwali wangwiro ndithu. Onani, zizindikiro zake ndi izi.” Apo adzaonetse chovala cha mkaziyo kwa akuluakuluwo. Tsono akuluakulu am'mudzimo amtenge mwamunayo ndi kumkwapula. Pambuyo pake amlipitsenso masekeli asiliva makumi khumi, ndipo azipereke kwa bambo wa mtsikanayo. Alipe ndithu chifukwa choti adanyozetsa mnamwali Wachiisraele amene sadamdziŵeko mwamuna. Komanso adzakhalabe mkazi wake ndithu, ndipo pa moyo wake wonse sadzathanso kumsudzula. Koma ngati zomunenerazo ndi zoona, ndipo umboni wakuti mtsikanayo adaali namwali wosadziŵa mwamuna ukusoŵa, pamenepo apite naye pakhomo pa bambo wake. Pomwepo amuna amumzindamo amuphe pakumponya miyala. Mtsikanayo wachita chinthu chochititsa manyazi pakati pa mtundu wathu wa Israele pochita zadama m'nyumba ya bambo wake. Motero mudzachotsa choipa pakati pa inu. Munthu akagwidwa akuchita chigololo ndi mkazi wa mwiniwake, aphedwe onsewo, mwamuna ndi mkazi yemwe. Choncho mudzachotsa choipa pakati pa inu. Tiyese kuti mwagwira munthu mumzinda momwemo akuchita chigololo ndi mnamwali wofunsidwa mbeta, amene sadamdziŵeko mwamuna. Muŵatenge onsewo, mupite nawo kunja kwa mzinda, ndipo muŵaphe poŵaponya miyala. Mtsikanayo aphedwe chifukwa ngakhale anali m'mudzi, sadakuwe kuti anthu adzamthandize. Mwamunayo aphedwe chifukwa wachimwa ndi mtsikana wofunsidwa mbeta ndi mnzake. Motero mudzachotsa choipa pakati panu. Mwina munthu, kuthengo koteroko, achita kugwirira mtsikana wofunsidwa mbeta nachita naye chigololo momkakamiza. Zikatero, munthu wamwamuna yekhayo ndiye aphedwe. Mtsikanayo musamchite kanthu chifukwa choti sadachite tchimo loyenera kufa nalo. Mlandu umenewu ukufanafana ndi wakuti munthu aputa mnzake, namupha. Munthuyo wachita kumgwira mtsikanayo nkuchita naye chigololo kuthengo. Ndipo ngakhale adaakuwa, panalibe amene akadampulumutsa. Mwina munthu agwidwa akugwirira mnamwali wosafunsidwa mbeta, amene sadamdziweko mwamuna, nachita naye chigololo momkakamiza. Munthuyo alipe bambo wake wa mtsikanayo mtengo wofunsira mbeta, ndiye kuti masekeli asiliva makumi asanu, ndipo amtenge kuti akhale mkazi wake chifukwa choti adamkakamiza kuchita naye chigololo. Tsono pa moyo wake wonse sangathenso kumsudzula. Munthu asakwatire mkazi wa bambo wake, kapena kuchita chipongwe chomuvula. Mwamuna aliyense wofulidwa, kapena woduka chiwalo chaumuna, asaloŵe mu msonkhano wa anthu a Chauta. Mwana wam'chigololo asaloŵe mu msonkhano wa anthu a Chauta, ngakhale zidzukulu zake mpaka mbadwo wachikhumi. Mwamoni kapena Mmowabu asaloŵe msonkhano wa anthu a Chauta. Ngakhale mdzukulu wao aliyense mpaka mbadwo wachikhumi, asaloledwe kuloŵa mu msonkhano wa anthu a Chauta. Iwoŵa sadakupatseniko chakudya kapena madzi pa ulendo wanu uja wochoka ku Ejipito. Ndipo adalemba ntchito Balamu, mwana wa Beori, wa m'mudzi mwa Petori ku Mesopotamiya, kuti akutemberereni. Koma Chauta, Mulungu wanu, sadamumvere Balamuyo. Matembererowo adaŵasandutsa madalitso pa inu, popeza kuti adakukondani inu. Pa masiku onse a moyo wanu musachite kanthu kalikonse kothandiza anthu a mitundu imeneyi, kuti apeze mtendere kapena ubwino. Musaŵanyoze Aedomu. Amene aja ndi abale anu. Musaŵanyoze Aejipito, popeza kuti kale mudaakhala m'dziko mwao. Kuyambira pa mbadwo wachitatu mpaka muyaya, zidzukulu zao zingathe kuloŵa nao mu msonkhano wa anthu a Chauta. Mukakhala m'zithando pa nthaŵi yankhondo, muzilewa zonse zimene zingathe kukulakwitsani. Ngati mwamana aliyense pakati panu waipitsidwa chifukwa chakuti wadzilotera usiku, atuluke m'zithando ndipo akhale kunja kwa zithandozo. Madzulo asambe ndithu, ndipo pomaloŵa dzuŵa, abwerere ku zithando. Kunja kwa zithando, mukonze malo kumene mungathe kumapitako kukadzithandiza. Mwa zida zanu muzitenga chokumbira, kuti muthe kukumba kadzenje komadzithandizirapo, tsono mutatha, mufotsere. Zithando zanuzo zizikhala zaukhondo, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, amayenda pakati pa zithando zanu, kuti akutchinjirizeni ndi kukupambanitsani kwa adani anu. Choncho m'zithando zanu mukhale mwabwino, kuti Chauta asaone kanthu kalikonse konyansa ndi kukufulatirani. Kapolo akathaŵa kwa mbuye wake, nkubwera kwa inu kuti mumsunge, musambweze kwa mbuyakeyo. Angathe kukhala pakati pa inu mu mzinda wanu uliwonse umene angasankhe ndiponso kumene kungamkomere, musamvute ai. Pakati pa ana a Aisraele pasakhale akazi kapena amuna okhala mahule a ku Nyumba ya Mulungu. Ndalama zozipeza mwa njira yadama yotereyi, yochitika ndi mkazi kapena mwamuna, musabwere nazo ku Nyumba ya Chauta, Mulungu wanu, kuti mukwaniritsire malonjezo anu, poti zimenezi Chauta, Mulungu wanu, amadana nazo. Mukakongoza mbale wanu ndalama, kapena chakudya kapena kanthu kena kalikonse, musamulipitse chiwongoladzanja pobweza. Mlendo yekha mungathe kumlipitsa chiwongoladzanja, koma osati mbale wanu. Lamulo limeneli mulimvere ndithu, ndipo Chauta, Mulungu wanu, adzadalitsa ntchito zanu zonse m'dziko limene mukukakhalamolo. Ukachita lonjezo kwa Chauta, Mulungu wako, usazengereze kuchita chimene walonjezacho. Chauta adzakuumiriza kuti uchichite, ndipo kuzengereza nkuchimwa. Koma ngati simulonjeza, apo palibe kulakwa ai. Choncho muzisunga mau amene adatuluka m'kamwa mwanu, chifukwa mudalonjeza mwaufulu kwa Chauta kuti mudzachitadi zimene mudalonjeza. Mukamayenda m'njira yodzera m'munda wamphesa wa mnzanu wokhala naye pafupi, mungathe kudyako mphesa zimene mungafune, koma musatengereko m'dengu pochoka. Mukayenda m'njira yodzera m'munda watirigu, mungathe kudyako ngala za tirigu mobudula ndi manja, koma musadule tirigu ndi chikwakwa m'munda mwa mnzanuyo. Tiyese kuti munthu wakwatira mkazi, pambuyo pake nkunena kuti mkaziyo sakumfuna, chifukwa choti wampeza cholakwa. Alembe kalata yachisudzulo, ndi kumpatsa mkaziyo pamanja, namchotsa pakhomo pake. Mkaziyo akakwatiwa ndi mwamuna wina, ndipo pambuyo pake winayonso nkunena kuti sakumfuna, angathe kumlemberanso kalata yachisudzulo nkumpatsa. Mkaziyo atachokapo pakhomopo, kapena mwamuna wachiŵiri uja atafa, mwamuna wake woyamba uja sayenera kumkwatiranso, ayenera kumuwona ngati woipitsidwa. Kumkwatiranso nkuchimwa pamaso pa Chauta. Tsono musaloŵemo ndi cholakwa m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo. Munthu akangokwatira kumene, musamlembe m'gulu la ankhondo, kapena kumpatsa ntchito ina iliyonse. Papite chaka chathunthu asanachite zimenezi, kuti choncho athe kukhala kwao ndi kumakondweretsa mkazi wake amene adamkwatirayo. Mukakongoza munthu kanthu, musamtengere mphero yake yoperera tirigu kuti ikhale pinyolo. Kumlanda chimenechi, ndiye kumchotsera chinthu chomuthandiza pa moyo wake. Aliyense woba Mwisraele mnzake ndi kumsandutsa kapolo kapena kumgulitsa ngati kapolo, aphedwe ndithu. Motero mudzachotsa choipa chimenechi pakati pa inu. Kunena za nthenda ya khate, muwone ndithu kuti mukutsatadi malangizo onse amene ndapatsa ansembe Achilevi, ana a Levi, kuti akuuzeni. Kumbukirani zimene Chauta, Mulungu wanu, adamchita Miriyamu, muja munkachokera ku Ejipitomu. Mukakongoza munthu kanthu, musaloŵe m'nyumba mwake kukatenga chovala chimene afuna kukupatsani ngati pinyolo. Inu mukhale panja, mwini wakeyo achite kukupatsani yekha. Ngati munthuyo ndi wosauka, chovala chapinyolocho chisakagone kwanu. Chibwezeni dzuŵa lisanaloŵe, kuti iye afunde usiku. Apo adzakuthokozani, ndipo Chauta, Mulungu wanu, adzakondwera nanu. Wantchito wolembedwa amene ali mmphaŵi ndi wosoŵa, musamamdyerera, ngakhale akhale mnansi wanu kapena mlendo wokhala mumzinda mwanu m'dziko lanulo. Tsiku lililonse dzuŵa lisanaloŵe, muzimlipira malipiro a tsikulo. Ndalamazo akuzisoŵa iyeyo ndipo akuŵerengera zomwezo. Mukapanda kumlipira, adzakulirirani kwa Mulungu ndipo mudzatsutsidwa kuti ndinu ochimwa. Makolo asafere zolakwa za ana ao. Momwemonso ana asafere zolakwa za makolo ao. Munthu aphedwe chifukwa cha zoipa za iye mwini. Alendo kapena ana amasiye musaŵalande zao zoŵayenera, poŵapotozera mlandu wao. Ndipo mkazi wamasiye musamlande chovala kuti chikhale pinyolo ya ngongole. Kumbukirani kuti paja mudaali akapolo ku Ejipito, ndipo kuti Chauta, Mulungu wanu, adakuwombolani kumeneko. Nchifukwa chake ndakupatsani lamulo limeneli. Mukamakolola dzinthu m'minda mwanu, zina pang'ono nkuiŵalika, musabwerere kukatenga zoiŵalikazo. Zimenezo muzisiyire alendo okhala nanu, ana amasiye ndi akazi amasiye, ndipo Chauta, Mulungu wanu, adzakudalitsani pa ntchito zanu zonse. Mutatha kukolola olivi koyamba, musapitemonso m'mitengomo kukatenga zotsala. Zimenezo ndi za alendo okhala nanu, za ana amasiye ndi akazi amasiye. Mutha kuthyola koyamba mphesa zanu, koma musapitemonso kachiŵiri m'mitengomo. Mphesa zotsalazo ndi za alendo okhala nanu, za ana amasiye ndi akazi amasiye. Mukumbukire kuti mudaali akapolo m'dziko la Ejipito. Nchifukwa chake ndakupatsani lamulo limeneli. Tiyese kuti anthu aŵiri akangana. Tsono atapita ku bwalo lamilandu, aweruzi nkugamula kuti uyu sadalakwe koma wolakwa ndi winayu. Ngati wolakwayo ayenera kukwapulidwa, muweruziyo amlamule kuti agone pansi ndipo akwapulidwe mikwapulo yolingana ndi kulakwa kwake. Angathe kumkwapula mpaka mikwapulo makumi anai, koma osapitirira pamenepo. Zikapitirira pamenepo, ndiye kuti zidzamchititsa manyazi mbale wanuyo. Ng'ombe imene ikupuntha tirigu, musaimange pakamwa. Abale aŵiri akamakhala pamodzi, ndipo wina nkumwalira, koma osasiya mwana, mkazi wamasiyeyo asakwatiwe ndi munthu wa banja lina. Mbale wake wa malemuyo amtenge, amkwatire ndipo apitirize ntchito ya mbale wake kwa mkazi ameneyo. Mwana woyamba kubadwa m'nyumbamo, adzakhala mwana wa mbale wake womwalirayo, kuti dzina la banja lake lisaferetu m'dziko la Israele. Koma ngati mbale wa malemuyo samufuna mkazi wa mbale wakeyo, mkaziyo angathe kupita ku chipata kwa akuluakulu ndi kukadandaula kuti, “mbale wa mwamuna wanga uja sakufuna kuti dzina la mbale wakeyo lipitirire m'dziko la Israele. Akukana kundiloŵa chokolo.” Pamenepo akuluakulu amumzindamo amuitane kuti alankhule naye. Akapitirira ndithu kukana kumkwatira, mkaziyo apite kwa mlamu wakeyo pamaso pa akuluakulu onsewo, ndipo amuvule nsapato yakumodzi, amthire malovu kumaso ndi kunena kuti, “Zimenezi ndiye zoyenera kumchitikira munthu wokana chokolo cha mbale wake.” M'dziko la Israele, banja la mwamunayo lidzatchedwa banja la munthu amene adamuvula nsapato yakumodzi. Anthu aŵiri akamamenyana ndipo mkazi wa mmodzi pofuna kupulumutsa mwamuna wake, agwira mdani wakeyo ku moyo, musamchitire chifundo mkazi ameneyo, mumdule dzanja. Miyeso yopimira kulemera musakhale nayo iŵiri m'thumba mwanu, waukulu ndi waung'ono. Miyeso yopimira kuchuluka musakhale nayo iŵiri m'nyumba mwanu, waukulu ndi waung'ono. Miyeso ikhale miyeso yeniyeni yabwino, kuti mukakhale nthaŵi yaitali m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsani. Chauta amadana ndi anthu onyenga mwa njira yotereyi. Kumbukirani zimene adakuchitani Aamaleke nthaŵi ija munkachoka ku Ejipitoyi. Analibe mantha ndi Mulungu. Motero adakuthirani nkhondo pa njira, pamene mudaali mutatheratu nkutopa. Paja adaŵapheratu anzanu onse amene ankachedwa ndi kuyenda m'mbuyo. Motero tsono, Chauta, Mulungu wanu, akadzakupatsani dziko kuti likhale choloŵa chanu, nadzakulanditsani m'manja mwa adani anu onse okuzungulirani, kasamaleni kuti mukaphe Aamaleke onse, kuti munthu asadzaŵakumbukenso mpang'ono pomwe. Musaiŵale zimenezi. Mukadzaloŵa ndi kukhazikika m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo, aliyense mwa inu pa zokolola zonse zoyamba zimene adazipeza m'dziko limene Chauta akukupatsanilo, atengeko zina ndi kuziika m'dengu, ndipo apite nazo ku malo amene Chauta, Mulungu wanu, adasankhula kuti anthu azidzapembedzerako. Apite kwa mkulu wa ansembe amene ali pa ntchito nthaŵi imeneyo, ndipo amuuze kuti, “Tsopano ndadziŵadi kuti Chauta, Mulungu wanga, wandiloŵetsa m'dziko limene adalonjeza makolo athu kuti adzatipatsa ife.” Wansembeyo ndiye amene adzakulandireni dengulo ndi kuliika patsogolo pa guwa la Chauta, Mulungu wanu. Tsono pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, muzidzanena kuti, “Kholo langa linali Lachiaramu, munthu wongoyendayenda, amene adapita ku Ejipito ndi banja lake nakakhala kumeneko. Popita kumeneko, anthuwo adaali ochepa, koma pambuyo pake adachuluka nasanduka mtundu waukulu ndi wamphamvu. Aejipito adatichita zankhanza ndi kutizunza potigwiritsa ntchito mwaukapolo. Pamenepo ife tidalirira Chauta, Mulungu wa makolo athu, kuti atithandize. Iyeyo adatimva, ndipo adaona kusauka kwathu, ntchito yolemetsa imene iwo aja ankatigwiritsa, ndiponso moyo wathu wopsinjidwawo. Mwa mphamvu zake zazikulu ndiponso ndi dzanja lake lotambalitsa, Chauta adatitulutsa ku Ejipito. Padaoneka zozizwitsa ndi zizindikiro, ndipo padachitika zinthu zoopsa zambiri. Potsiriza adatifikitsa kuno, natipatsa dziko lino, dziko lamwanaalirenji. Motero tsopano, ndikubwera kwa Chauta ndi gawo la zokolola zoyamba za m'dziko limene wandipatsa.” Apo mutatula pansi dengulo pamaso pa Mulungu, mumpembedze pomwepo. Kondwani popeza kuti Chauta, Mulungu wanu, wakupatsani zabwino, inu ndi a m'banja mwanu. Mukondwe inu ndi Alevi, ndiponso alendo amene mumakhala nawo. Chaka chachitatu chilichonse muzipereka chopereka chachikhumi cha zokolola zanu kwa Alevi, alendo, ana amasiye ndi akazi amasiye, kuti kumizinda kumene amakhala iwoŵa, adzakhale ndi chakudya chokwanira. Mutachita zimenezi, munene kwa Chauta kuti, “Palibe nchimodzi chomwe chopereka chachikhumi chimene chatsalako m'nyumba mwanga. Zonse ndapereka kwa Alevi, alendo, ana amasiye ndi akazi amasiye, monga mudandilamulira. Sindidanyoze kapena kuiŵalapo malamulo anu ndi limodzi lomwe. Pa za chachikhumi sindidadyepo nchimodzi chomwe pamene ndinkalira maliro. Pamene ndinali woipitsidwa pa zachipembedzo, sindidagwirepo nchimodzi chomwe. Ndipo sindidaperekepo nchimodzi chomwe kuperekera anthu akufa. Inu Chauta, Mulungu wanga, ndakumverani. Zonse zimene mudalamula za chopereka chachikhumi ndachita. Yang'anani pansi kuchokera kumwambako ku malo anu oyera, ndipo mudalitse anthu anu Aisraele. Mudalitsenso dziko ili lamwanaalirenji limene mwatipatsali, monga momwe mudalonjezera makolo athu.” Chauta, Mulungu wanu, akukulamulani lero lino kuti mumvere malangizo ndi malamulo ake. Tsono muŵamveredi ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse. Lero mwamdziŵa Chauta kuti ndi Mulungu wanu. Mwalonjeza kumvera Iyeyo, kusunga malangizo ndi malamulo ake, ndi kuchita zonse zimene akulamulani. Lero Chauta wakulandirani ngati anthu ake, monga momwe adakulonjezerani, malinga nkusunga malamulo ake onse. Motero pa matamando, pa mbiri ndi pa ulemerero adzakukwezani kupambana mitundu ina yonse ya anthu imene adailenga, ndipo mudzakhala anthu ake oyera mtima, monga momwe adalonjezera. Pambuyo pake Mose, ali pamodzi ndi akuluakulu a Aisraele adauza anthu kuti, Muzimvera malamulo onse omwe ndikukupatsani leroŵa. Pa tsiku limene muzaoloke mtsinje wa Yordani ndi kuloŵa m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsani, mudzaimiritse miyala yaitali, ndipo mudzaikulungize. Mutatero, mudzalembepo mau onse a malamulo ameneŵa, mukakaloŵa m'dziko lamwanaalirenjilo, limene Chauta, Mulungu wa makolo anu, adakulonjezani. Mutaoloka Yordani, mudzaimiritse miyala imeneyi pa phiri la Ebala, monga momwe ndakulamulirani lero, ndipo mukaikulungize. Kumeneko mukamangeko guwa la Chauta, Mulungu wanu, guwa la miyala yosasema ndi chitsulo chilichonse. Guwalo likhale la miyala yosasema. Muzikapereka pamenepo nsembe zopsereza kwa Chauta, Mulungu wanu. Ndipo muzikaphera ndi kudyera nsembe zachiyanjano komwekonso, ndi kumakhala okondwa pamaso pa Chauta, Mulungu wanu. Pamiyalapo mudzalembepo mau onse a malamulo ameneŵa mooneka bwino. Pamenepo Mose pamodzi ndi ansembe Achilevi adauza Aisraele kuti: Mverani inu Aisraele, ndipo tcherani khutu. Lero mwasanduka anthu ake a Chauta, Mulungu wanu. Tsono mumvereni, ndipo musunge malamulo ndi malangizo ake onse amene ndikukupatsani leroŵa. Tsiku lomwelo Mose adauza Aisraele kuti, Mukangooloka Yordani, mafuko amene adzaima pa phiri la Gerizimu, pamene madalitso adzatchulidwa pa Aisraele, ndi aŵa: Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, Yosefe ndi Benjamini. Koma mafuko ena amene adzaimirire pa phiri la Ebala, pamene matemberero adzatchulidwe pa Aisraele, ndi aŵa: Rubeni, Gadi, Asare, Zebuloni, Dani ndi Nafutali. Ndipo Alevi azidzanena mau aŵa mokweza kuti, “Atembereredwe aliyense wopanga fano losema kapena loumba, namalipembedza mobisa. Chauta amanyansidwa nacho chinthu chopanga mmisiricho.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!” “Atembereredwe aliyense wosalemekeza atate ndi amai ake.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!” “Atembereredwe aliyense wosuntha malire a mnansi wake.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!” “Atembereredwe aliyense wosokeza munthu wakhungu.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!” “Atembereredwe aliyense woweruza mopotoza milandu ya alendo, ya ana amasiye, ndi ya akazi amasiye.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!” “Atembereredwe aliyense wogona ndi mkazi wa bambo wake, chifukwa wavula mkazi wa bambo wake.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!” “Atembereredwe aliyense wogona ndi nyama.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!” “Atembereredwe aliyense wogona ndi mlongo wake, kapena mlongo wake wa mimba ina.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!” “Atembereredwe aliyense wogona ndi mpongozi wake.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!” “Atembereredwe aliyense wopha mnzake mwachinsinsi.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!” “Atembereredwe onse olandira chiphuphu kuti aphe munthu wosalakwa.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!” “Atembereredwe aliyense wosavomereza ndi wosatsata malamulo amene tatchulaŵa.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!” Mukamamvera mau a Chauta, Mulungu wanu, ndi kutsata mosamala malamulo onse amene ndikukupatsani leroŵa, Chauta, Mulungu wanu, adzakukwezani kopambana mitundu yonse ya pa dziko lapansi. Mverani Chauta, Mulungu wanu, ndipo mudzalandira madalitso onse aŵa: Chauta adzadalitsa mizinda yanu ndi minda yanu. Chauta adzadalitsa ana anu ndi zokolola zanu, ndi ana a zoŵeta zanu, ndipo adzakupatsani ng'ombe ndi zoŵeta zina zambiri. Chauta adzadalitsa mbeu zanu ndi chakudya chimene muchikonza kuchokera ku mbeuzo, kuti zichuluke. Chauta adzadalitsa zochita zanu zonse. Chauta adzakuthandizani kuti mugonjetse adani anu pamene akuukirani. Pokuukirani adzatulukira njira imodzi, koma pothaŵa adzathaŵira m'zikuŵa zisanu ndi ziŵiri. Chauta adzadalitsa ntchito zanu, ndipo nkhokwe zanu zidzadzaza. Adzakudalitsani m'dziko limene akukupatsanilo. Chauta adzakusandutsani anthu opatulikira Iye monga adalonjezera, malinga mukachita zonse zimene akukulamulani ndi kuyenda m'njira yake. Tsono anthu onse a pa dziko lonse lapansi adzaona kuti Chauta, Mulungu wanu, wakusankhani inu kuti mukhale anthu akeake, ndipo azidzakuwopani. Chauta adzakudalitsani pokupatsani ana ambiri, zoŵeta zambiri ndiponso zokolola zambiri. Zonsezi adzakupatsani m'dziko limene Iye adalonjeza kwa makolo anu kuti adzakupatsani. Pa nyengo yake, adzakutumizirani mvula kuchokera kumene amaisunga mu mlengalenga, ndipo adzadalitsa ntchito zanu zonse, kotero kuti inuyo muzidzakongoza mitundu ina zinthu, koma inuyo osakongola kwa aliyense. Mulungu wanu adzakusandutsani atsogoleri pakati pa mitundu ya anthu, osati otsata pambuyo. Mukamamvera malamulo ake amene ndikukupatsani lero ndi kuŵatsatadi mosamala, mudzakhala okwera nthaŵi zonse, osati otsika. Choncho pa mau ndikukuuzani leroŵa, musapatuke kumanja kapena kumanzere, pakutsata milungu ina ndi kumaitumikira. Komatu mukapanda kumvera bwino mau a Chauta, Mulungu wanu, ndi kutsata malamulo ndi malangizo amene ndikukupatsani lero lino, adzakugwerani matemberero aŵa: Chauta adzatemberera mizinda yanu ndi minda yanu. Chauta adzatemberera zokolola zanu ndiponso zokandiramo ufa wanu. Chauta adzakutembererani pokupatsani ana oŵerengeka, zokolola zochepa, ndiponso ng'ombe ndi zoŵeta zina pang'ono chabe. Chauta adzatemberera ntchito zanu zonse. Mukamachita zoipa ndi kumkana Mulungu, Iye adzakutumizirani matemberero, chisokonezo ndiponso zokuvutani pa ntchito zanu zonse, mpaka mutaonongeka ndi kufa nonsenu pa kamphindi kochepa. Adzakutumizirani matenda otsatanatsatana, mpaka mutatha nonse kuti psiti m'dziko limene muli kukakhalamolo. Chauta adzakukanthani ndi nthenda zopatsana, zotupatupa ndi zamalungo. Adzakutumiziraninso kutentha koopsa ndi chilala ndiponso chinsikwi ndi chinoni zoononga mbeu zanu. Masoka amenewo adzakhala pa inu mpaka kukufetsani. Mvula sidzakugwerani ndipo nthaka yanu idzauma kuti gwa ngati chitsulo. M'malo mwa mvula, Chauta adzakugwetserani fumbi ndi mchenga, mpaka mutaonongeka nonse. Chauta adzalola kuti adani anu akugonjetseni. Pokalimbana nawo mudzadzera njira imodzi, koma poŵathaŵa mudzapanga zikuŵa zisanu ndi ziŵiri. Ndipo mafumu onse a pa dziko lapansi adzaopsedwa poona zokuchitikiranizo. Mutafa, mbalame pamodzi ndi nyama zakuthengo zidzadya mitembo yanu, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adzazipirikitse. Chauta adzakulangani ndi zithupsa zonga za ku Ejipito zija. Mudzakhala ndi zilonda, mphere, ndi kunyerenyesa, zonsezo zosamva mankhwala. Thupi lanu lidzakhala la mphere zokhazokha, ndipo muzidzangokandakanda, koma osachira. Chauta adzakuchititsani misala, ndipo adzakusandutsani akhungu ndi osokonezeka. Ngakhale dzuŵa lili nye, muzidzachita kufufuza njira ngati anthu akhungu. Kalikonse kamene mudzachite simudzalemera nako. Kaŵirikaŵiri azidzakupsinjani ndi kumakuberani, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adzakuthandizeni. Mudzafunsira mbeta mtsikana, koma ndi wina amene adzakwatirane naye. Kumanga nyumba mudzamanga ndithu, koma simudzagonamo. Munda wamphesa mudzabzala, koma mphesa zake simudzadyako. Ng'ombe zanu azidzakupherani mukupenya, koma nyama yake simudzadyako. Abulu anu azikaŵalanda mwamphamvu ndi kupita nawo kwina, inu mukupenya, ndipo sadzakubwezerani. Nkhosa zanu adzazipereka kwa adani anu, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adzakuthandizeni. Ana anu aamuna ndi aakazi adzatengedwa ukapolo ndi alendo, inu mukupenya. Tsiku ndi tsiku maso anu adzakhala ali psuu kuyang'anira ngati ana anuwo abwere, koma simudzaphulapo kanthu. Mtundu wachilendo udzakulandani zakumunda zanu zonse zimene mudathyoka nazo msana polima, ndipo mudzapsinjidwa ndi kuzunzika mosalekeza. Zimene mudzaziwona ndi maso zidzakupengetsani. Chauta adzabweretsa zilonda zoŵaŵa ndi zosachizika pa maondo ndi pamisongolo panu, ndipo anamkalimbwi azidzakutulukani thupi lonse, kuyambira kuphazi mpaka kumutu. Chauta adzaipirikitsira ku dziko lachilendo mfumu yanu, pamodzi ndi inu nomwe, kumene inuyo ndi makolo anu simudakhaleko nkale lonse. Kumeneko muzikatumikira milungu ina yopanga ndi mitengo ndi miyala. Ku mitundu yonse kumene Chauta adzakumwazireniko, anthu adzadabwa nanu, adzakusekani, adzakupekani nthano yokunyodolani. Mudzabzala zambiri, koma mudzakolola pang'ono chabe, chifukwa dzombe lidzadya zolima zanuzo. Minda yamphesa mudzalimadi, mpaka kuisamala bwino, koma mphesa zake simudzathyola kapena kumwako vinyo wake, chifukwa tizilombo ndito tidzadye mphesazo. Mitengo ya olivi izidzamera paliponse m'dziko mwanumo, koma mafuta a olivi simudzakhala nawo, chifukwa zipatso za olivizo zidzayoyoka. Mudzabereka ana aamuna ndi aakazi ndithu, koma sadzakhala anu, chifukwa adzatengedwa ukapolo. Mitengo yanu yonse ndi dzinthu dzanu dzam'munda zidzatha ndi tizilombo. Alendo okhala m'dziko mwanu ndiwo amene azidzakwererakwerera, koma inu muzidzatsikiratsikira. Iwowo azidzakukongozani ndalama, koma inu simudzakhala nazo ndi pang'ono pomwe zoŵakongoza, ndipo potsiriza adzakulamulirani. Masoka onseŵa adzakugwerani. Adzakhala pa inu mpaka mutaonongeka, chifukwa choti simudamvere Chauta, Mulungu wanu, ndipo simudatsate malamulo ndi malangizo onse amene Iye adakupatsani. Masoka onseŵa adzakhala mboni yapadera ya chilango cha Mulungu pa inu ndi pa zidzukulu zanu mpaka muyaya. Paja Chauta adakudalitsani pa zonse, komabe inu simudamtumikire mokondwa ndi mitima yachimwemwe. Motero mudzatumikira adani odzalimbana nanu amene Chauta adzakutumizireni. Mudzamva njala ndi ludzu. Zinthu zonse zidzakusoŵani pamodzi ndi zovala zomwe. Chauta adzakuzunzani mwankhanza, mpaka mutaonongeka. Chauta adzaitanitsa mtundu wa anthu ochokera ku malekezero a dziko lapansi, kuti adzamenyane nanu. Anthu a mtundu umenewo amene inu simudziŵa chilankhulo chao, adzakuterani ngati mphungu. Anthuwo adzakhala aukali, ndipo sadzachita chifundo ndi aliyense, ngakhale akhale mwana kapena nkhalamba. Adzakudyerani ng'ombe zanu pamodzi ndi zakumunda zanu zomwe, mpaka mudzafa ndi njala. Sadzakusiyiraniko mpang'ono pomwe tirigu, vinyo, mafuta aolivi, ng'ombe kapena nkhosa, ndipo mudzafadi. Adzathira nkhondo mzinda uliwonse, m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo. Ndipo malinga ataliatali amene mukuŵakhulupirirawo adzagwa ponseponse. Adzakuzingani m'mizinda yonse ya m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, adzakupatsanilo. Nthaŵi imene adani anu adzazinga mizinda yanu ndi kukusautsani koopsa, mudzasoŵa chakudya kotheratu, kotero kuti muzidzadya ana anu omwe aamuna ndi aakazi, amene Chauta adakupatsani. Ngakhale munthu amene ali woleredwa bwino ndi wofatsa mtima kwambiri mwa inu, adzamana chakudya mbale wake, mkazi wake wapamtima ndi ana ake omutsalira, mwakuti sadzapatsako ndi mmodzi yemwe nyama ya ana ake amene akuŵadya, chifukwa adzakhala alibiretu chakudya pa nthaŵi imene adani anu azidzakuzingani ndi kukusautsani koopsa. Ngakhale mkazi woleredwa bwino ndi wolobodoka kotero kuti sangayese nkomwe kupondetsa pansi phazi lake, adzamana mwamuna wake wapamtima ndi ana ake onse nyama ya ana ake ongobadwa kumene, pamodzi ndi za matenda ake zomwe zochokera m'mimba mwake, popeza kuti azidzadya zimenezi yekha mobisa, chifukwa cha kusoŵeratu chakudya, nthaŵi imene adani anu adzazinga mizinda yanu ndi kukusautsani kwambiri. Muzimvera mau onse a malamulo aŵa a m'buku muno, ndipo dzina ili lodabwitsa ndi lochititsa mantha la Chauta, Mulungu wanu, muzilitamanda. Mukapanda kutero, inuyo ndi zidzukulu zanu, Chauta adzakugwetserani masautso apadera, mavuto aakulu okhalitsa ndiponso nthenda zoopsa zosamva mankhwala. Nthenda zonse zoopsa zimene mudaopsedwa nazo muli ku Ejipito kuja, Chauta adzakugwetserani zimenezo, ndipo simudzachira. Adzakugwetseraninso nthenda zonse zamitundumitundu pamodzi ndi miliri yomwe, zimene sizidatchulidwepo m'buku la malamulo a Mulungu, ndipo mudzaonongeka. Ngakhale mudaachuluka ngati nyenyezi zakuthambo, koma amoyo mudzakhala ochepa, chifukwa choti simudamvere Chauta, Mulungu wanu. Monga momwe kudakomera Chauta kukudalitsani ndi kukuchulukitsani kuti mukhale ambiri, momwemo kudzamkomeranso kuti akuwonongeni kotheratu. Adzakuchotsani m'dziko limene mukuliloŵa kukakhalamolo. Ndipo Chauta adzakumwazani pakati pa mitundu yonse, kuyambira ku malekezero ena a dziko mpaka ku malekezero ake enanso. Kumeneko muzidzapembedza milungu yamitengo ndi yamiyala, imene inu ndi makolo anu simudaidziŵe nkale lonse. Simudzapeza mtendere kwina kulikonse ndipo malo anuanu simudzaŵapeza. Mudzakhala ankhaŵa, osoŵa thandizo ndi otaya mtima, ndipo Chauta ndiye adzagwetse zimenezi pa inu. Nthaŵi zonse, moyo wanu udzakhala wopenekapeneka. Muzidzakhala amantha, usiku ndi masana womwe, ndipo muzidzangokhalira kuwopa imfa. Mitima yanu idzakhala yamantha poona kalikonse. M'maŵa mulimonse muzidzangofuna kuti kude. Madzulo aliwonse muzidzafuna kuti kuche. Ndipo Chauta adzakutumizaninso ku Ejipito m'zombo zapanyanja, ngakhale kuti ndidaalonjeza kuti simudzapitakonso. Kumeneko mudzayesayesa kudzigulitsa ngati akapolo kwa adani anu, koma palibe ndi mmodzi yemwe amene adzafune kukugulani. Aŵa ndi mau a chipangano chimene Chauta adalamula Mose kuti achite ndi Aisraele m'dziko la Mowabu. Mau achipangano ameneŵa adangoonjezeka pa mau aja achipangano amene Chauta adaachita ndi iwowo ku phiri la Horebu kuja. Mose adaitana Aisraele onse aja, naŵauza kuti: Paja mudadziwonera nokha zimene Chauta adachita mfumu ya ku Ejipito ndi nduna zake ndi dziko lake lonse. Mudaonanso miliri yoopsa ija, zozizwitsa zija ndi zodabwitsa zimene adachita. Koma mpaka tsopano, Chauta sadakupatseni mtima womvetsa zinthu zimenezi, kapena maso openya, kapena makutu akumva. Pa zaka makumi anai zimene Chauta adakutsogolerani m'chipululu muja, zovala zanu sizidathe, ndipo nsapato zanu sizidang'ambike. Munalibe buledi woti muzidya, ngakhalenso vinyo kapena chakumwa chaukali, koma Chauta adakupatsani zonse zokusoŵani, kuti mudziŵe kuti Iye ndi Chauta, Mulungu wanu. Ndipo titafika pa malo ano, mfumu Sihoni wa ku Hesiboni, pamodzi ndi mfumu Ogi wa ku Basani, adadza kuti alimbane nafe, koma tidaŵagonjetsa. Tidalanda dziko lao ndi kuligaŵira mafuko a Rubeni, Gadi ndiponso hafu la fuko la Manase. Mau onse a chipangano ichi muŵamvere mokhulupirika, kuti choncho mudzakhoze pa zonse zimene mudzachite. Lero lino, nonse mukuimirira pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, atsogoleri anu, akuluakulu anu, akalonga anu, anthu aamuna a Aisraele, zidzukulu zanu, akazi anu ndiponso alendo amene amakhala m'mahema mwanu, amene amakudulirani nkhuni ndi kumakutungirani madzi. Muli pano lero kuti mulumbire ndi kuchita chipangano chimene Chauta, Mulungu wanu, akupangana nanu. Motero, mudzakhala anthu a Chauta, ndipo Iyeyo adzakhala Mulungu wanu, monga momwe adalonjezera kwa inu ndi kulumbira kwa makolo anu, Abrahamu, Isaki ndi Yakobe. Sindinu nokha amene Chauta akupangana nanu chipangano ichi chochita ndi malumbiro. Chipangano chimenechi akupangana ndi munthu aliyense amene ali pano lero pamaso pa Chauta, Mulungu wathu, ndiponso ndi ena onse amene sali nafe kuno lero. Mukudziŵa m'mene tidakhalira ku Ejipito kuja, ndiponso m'mene unaliri ulendo poyenda pakati pa maiko a mitundu ina. Mafano ao oipa amitengo, amiyala, asiliva ndiponso agolide, amene anali pakati pao, mudaona kunyansa kwake. Chonde muchenjere kuti mwamuna kapena mkazi, ngakhale banja, kaya fuko, kungoti nonsenu amene muli pano lero lino, musapotoloke kuti muchoke kwa Chauta, Mulungu wanu, ndi kumapembedza milungu ya anthu a mitundu ina. Kuteroko kungofanafana ndi muzu umene umati ukakula, umasanduka chiphe. Chonde muchenjere kuti pasakhale wina pano lero, womva mau ameneŵa, komabe namanena mumtima mwake kuti zinthu zidzamuyenderabe bwino, ngakhale akhale wokanika chotani nkumachita zake. Zimenezi zidzangoputira nonsenu chiwonongeko, abwino ndi oipa omwe. Munthu wotere Chauta sadzamkhululukira. Ndithu Chauta adzamkwiyira ndi nsanje yoyaka. Matemberero olembedwa m'buku muno adzamgwera ndipo Chauta adzamuwonongeratu ndipo adzaiŵalika pa dziko. Chauta adzampatula pakati pa anthu a ku Israele onse ndipo adzamlanga ndi masoka potsata matemberero a chipangano olembedwa m'buku lino la malamulo. Anthu a mibadwo yanu yakutsogolo, monga zidzukulu zanu ndi alendo ochokera kutali, adzaŵapenya masoka amenewo, pamodzi ndi masautso amene Chauta adzagwetse pa dziko lanu. Minda yanu idzakhala yoguga, yodzaza ndi sulufule ndi mchere. M'minda imeneyo simudzamera kalikonse, ngakhale ndi udzu womwe. Dziko lanu lidzakhala ngati mizinda ija ya Sodomu ndi Gomora, ndiponso ya ku Adima ndi Zoboimu, imene Chauta adaononga pa nthaŵi imene anali wokwiya koopsa ija. Tsono dziko lonse lapansi lidzafunsa kuti, “Kodi chifukwa chiyani Chauta adachita zotere m'dziko lake? Kodi chifukwa chake chinali chiyani kuti mkwiyo wake uchite kuwopsa chotere?” Yankho la mafunso onseŵa lidzakhala lakuti, “Chifukwa chake nchakuti anthuŵa adaphwanya chipangano chimene adachita ndi Chauta, Mulungu wa makolo ao, nthaŵi imene Iyeyo adaŵatulutsa ku Ejipito. Adatumikira milungu ina imene sadaipembedzepo nkale lonse, milungu imene Chauta adaŵaletsa kuipembedza. Motero Chauta adakwiyira anthu ake, ndipo adaŵagwetsera masoka onse olembedwa m'buku muno. Chauta adakwiya koopsa, ndipo ali wokwiya chotero, adaŵachotseratu m'dziko lao ndi kuŵaponya m'dziko lachilendo, kumene ali lero lino.” Pali zinthu zina zimene Chauta, Mulungu wathu, sanatiululire; koma watiululira ifeyo ndi zidzukulu zathu malamulo ake amene tiyenera kuwamvera nthaŵi zonse. Pamene adzakufikirani madalitso ndi matemberero amene ndatchula aja, mudzaŵakumbukira muli pakati pa mitundu ina kumaiko kumene Chauta, Mulungu wanu, adakumwazirani. Tsono inuyo ndi zidzukulu zanu mudzabwerera kwa Chauta, ndipo mau ake amene ndikukupatsani leroŵa mudzaŵamvera ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse. Pamenepo Chauta, Mulungu wanu, adzakukhazikaninso pabwino ndi kukuchitirani chifundo. Adzakusokolotsani kukuchotsani ku mitundu ina ya anthu, kumene adakumwaziraniko, ndipo adzakusandutsaninso olemera. Ngakhale mutamwazikira ku malekezero a dziko lapansi, Chauta, Mulungu wanu, adzakusonkhanitsani komweko nadzakutengani kuchokera kumeneko. Adzakuperekezani ku dziko limene makolo anu anali nalo kale, kuti mukakhazikikeko ndinu. Ndipo adzakupezetsani bwino ndi kukuchulukitsani kopambana m'mene adaaliri makolo anu. Chauta, Mulungu wanu, adzakupatsani inu ndi zidzukulu zanu mtima womvera, kotero kuti muzidzamkonda ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse. Motero mudzakhalabe ndi moyo m'dziko limenelo. Koma Chauta, Mulungu wanu, adzagwetsa matemberero onse aja pa adani anu amene adakuzunzani. Inuyo mudzamveranso ndi kumatsata malamulo amene ndikukupatsani leroŵa. Chauta adzakupezetsani bwino pa zochita zanu zonse. Mudzakhala ndi ana ambiri, zoŵeta zambiri, ndipo minda yanu idzakubalirani zokolola zambiri. Adzakondwera nanu kuti mwakhoza chotere, monga momwe adakondwera ndi makolo anu pamene anali okhoza. Komatu muzidzamvera Chauta, Mulungu wanu, ndi kusunga malamulo ndi malangizo ake onse amene ali m'buku lino la malamulo ake. Mutembenukire kwa Iye ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse. Lamulo ndikukupatsani leroli si lovuta kulimvetsa ndipo si lapatali. Silili kumwamba, kuti muzichita kudzifunsa kuti, “Kodi amene akwere kumwamba kukatitsitsira lamulo kuti tilimve, ndani?” Komanso silili pa tsidya la nyanja, kuti muthe kufunsa kuti, “Kodi amene aoloke nyanja kukatitengera lamulo kuti tilimve, ndani?” Muli nalo pompano. Mukulidziŵa, mumalitchula ndipo mungathe kulitsata. Ndikukupatsani mpata lero woti musankhe, kapena moyo ndi zabwino, kapena imfa ndi zoipa. Mukamamvera malamulo a Chauta, Mulungu wanu, ndi malangizo ake amene ndikukupatsani lero, mukamamkonda Chauta, Mulungu wanu ndi kutsata mau ake onse, pamenepo mudzakhala pabwino ndipo mudzakhala mtundu wa anthu ochuluka. Chauta, Mulungu wanu, adzakudalitsani m'dziko mukukakhalamolo. Koma mukapanda kumvera, mukamakana kumva, m'malo mwake nkumatengeka kuti mupembedze milungu ina, ndikuchenjezeranitu tsopano kuti mudzaonongeka. Dziko ili la patsidya pa Yordani limene mukupita kukakhalamolo, simudzakhalitsamo. Tsopano ndikukupatsani mpata woti musankhe, kapena moyo kapena imfa, madalitso a Mulungu kapena matemberero ake. Zonse zakumwamba ndi zapansi zikhale mboni za zimene ndakuuzani lerozi. Tsono sankhani moyo, mukonde Chauta, Mulungu wanu, muzimvera mau ake ndi kukhala okhulupirika kwa Iye, kuti inu ndi zidzukulu zanu mudzakhalitsemo m'dziko limene adalonjeza kuti adzapatsa makolo anu, Abrahamu, Isaki ndi Yakobe. Mose adapitirira kulankhula ndi Aisraele aja kuti: Tsopano ndili ndi zaka 120, ndipo sindingathenso kukhala mtsogoleri wanu. China nchakuti Chauta adandiwuza kuti Yordaniyu sindimuwoloka. Mwini wake Chauta, Mulungu wanu, ndiye amene adzakuperekezeni ndi kuwononga mitundu ina yonseyi, kuti inu mukhale m'dziko mwao. Yoswa adzakhala mtsogoleri wanu, monga momwe Chauta wanenera. Chauta adzaŵaononga anthu ameneŵa monga momwe adaonongera Sihoni ndi Ogi, mafumu a Aamori, pamodzi ndi dziko lao. Chauta adzakupambanitsani, ndipo adaniwo muzikaŵachita zomwe ndakulamulanizi. Khalani amphamvu ndiponso mulimbe mtima. Musaŵaope anthu ameneŵa, musachite nawo mantha, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, adzakhala nanu. Sadzalola kuti mulephere, ndipo sadzakusiyani. Pomwepo Mose adaitana Yoswa pamaso pa Aisraele onse ndipo adamuuza kuti, “Khala wamphamvu ndipo ulimbe mtima. Ndi iweyo amene udzatsogolere anthu aŵa ku dziko limene Chauta adalonjeza makolo ao. Ndiwe amene udzakhazikitsa anthu m'dzikomo. Chauta mwini wake adzakutsogolera, ndipo adzakhala nawe. Sadzalola kuti ulephere, ndipo sadzakusiya. Motero usachite mantha kapena kutaya mtima.” Pamenepo Mose adalemba malamulo a Mulungu ndi kuŵapatsa ansembe, ana a Levi, amene ankanyamula Bokosi lachipangano la Chauta. Adaŵapatsanso atsogoleri a Aisraele. Adaŵalamula onsewo kuti, “Kamodzi pa zaka zisanu ndi ziŵiri zilizonse, pamene chaka cha kumasulidwa chafika, muŵerenge malamuloŵa pa chikondwerero cha misasa. Muŵaŵerenge kwa Aisraele onse, pamene adzabwere kudzapembedza Chauta pa malo oŵasankha Iyeyo. Mudzaitane amuna onse, akazi, ana ndi alendo amene ali m'mizinda mwanu, kuti aliyense adzimvere yekha, ndipo aphunzire kuwopa Chauta, Mulungu wanu, ndi kumamvera mau ake mosamala. Mwa njira imeneyi zidzukulu zanu zimene sizidamve malamulo a Chauta nkale lomwe, zidzamva, ndipo zidzaphunzira kuwopa Chauta nthaŵi yonse imene zidzakhale m'dziko limene mukukakhalamolo patsidya pa Yordani.” Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Nthaŵi ya moyo wako yatsala yochepa. Itana Yoswa, ubwere naye ku chihema chamsonkhano kuti ndimulangize.” Mose pamodzi ndi Yoswa adapita ku chihema chamsonkhano, ndipo Chauta adaŵaonekera iwowo mu mtambo wonga chipilala umene udaaima pakhomo pa chihemacho. Pambuyo pake Chauta adauza Mose kuti, “Patsala pang'ono kuti iwe umwalire. Ndiye iwe ukapita, anthuŵa adzaphwanya chipangano chomwe ndidachita nawo. Adzandisiya Ine, nkumapembedza milungu ya dziko limene akukakhalamolo. Zikadzangotero, ndidzaŵakwiyira ndi kuŵasiya, ndipo adzatheratu. Masoka ndi zoipa zina zambiri zidzaŵagwera. Tsono masiku amenewo azidzanena kuti, ‘Kodi zoipazi sizikutigwera chifukwa chakuti Chauta, Mulungu wathu, sali nafenso?’ Ndithudi pa nthaŵi imeneyo ndidzaŵafulatira chifukwa cha machimo onse amene iwo adachita popembedza milungu ina. “Tsopano talemba nyimbo iyi. Uŵaphunzitse ndi kuŵalimbitsa Aisraele kuti idzakhale mboni yanga yoŵatsutsa. Ndidzaŵaloŵetsa m'dziko lamwanaalirenji, monga momwe ndidalonjezera makolo ao. Kumeneko adzapeza chakudya chonse chomwe angachifune, ndipo adzakhala mosangalala. Komabe adzatembenukira ku milungu ina ndi kumaipembedza. Adzandikana Ine, ndipo adzaphwanya chipangano changa. Choncho masoka oopsa adzaŵagwera. Nyimbo imeneyi idzakhala mboni yanga yoŵatsutsa, chifukwa zidzukulu zao zizidzaiimba. Ngakhale tsopano lino ndisanaŵaloŵetse m'dziko limene ndidalumbira kuti ndidzaŵapatsa, ndikudziŵa zimene iwo akulingalira.” Tsiku lomwelo Mose adalemba nyimbo naphunzitsa Aisraele. Tsono Chauta adauza Yoswa, mwana wa Nuni, kuti, “Khala wamphamvu ndipo ulimbe mtima. Udzaŵatsogolera Aisraele kukaloŵa m'dziko lomwe ndidaŵalonjeza. Ndipo ndidzakhala nawe.” Tsono Mose adalemba malamulo a Mulungu m'buku, osasiya kanthu. Atamaliza, adauza Alevi amene ankanyamula Bokosi lachipangano kuti, “Tengani buku ili la malamulo a Mulungu, ndipo muliike pambali pa Bokosi lachipangano la Chauta, Mulungu wanu, kuti likhale kumeneko ngati mboni yokutsutsani. Ndikudziŵa kukanika kwanu ndiponso uchigaŵenga wanu. Ngati mugalukira Chauta, ndikadali moyo, nanji ndikadzafa, ndiye mudzaposa kugaluka kwake. Mundisonkhanitsire atsogoleri onse a mafuko pamodzi ndi akuluakulu omwe, kuti ndiŵauze zimenezi. Kumwamba ndi dziko lapansi ndizo zidzakhale mboni zoŵatsutsa. Ndikudziŵa kuti ine ndikadzafa, nonse mudzaipa ndipo mudzakana zimene ndakuuzanizi. Koma pambuyo pake kutsogoloko, mudzakomana ndi masoka, chifukwa chochita zoipa pamaso pa Chauta ndi kuputa mkwiyo wake pakuchulukitsa machimo anu. Mwakwiyitsa Chauta pochita zimene Iyeyo amakana.” Tsono Mose adanena mau a nyimbo yonseyi, kuyambira poyamba mpaka potsiriza, Aisraele onse alikumva: Dziko lakumwamba, imva zimene ndikuti ndilankhule. Dziko lapansi imva mau a pakamwa panga. Zophunzitsa zanga zigwe ngati mvula, mau anga atsike ngati mame, ngati mvula yowaza pa msipu wanthete, ngati mvula yamphamvu pa udzu watsopano. Ndidzatamanda dzina la Chauta. Tamandani ukulu wake wa Mulungu. Chauta ndi Thanthwe, ntchito zake ndi zangwiro, njira zake zonse ndi zolungama, ndi Mulungu wokhulupirika ndi wosaipa konse, wachilungamo ndi wosalakwa. Koma inu ndinu osakhulupirika, osayenera kukhala anthu ake, ndinu mtundu wochimwa ndi wonyenga. Inu anthu opusa ndi opanda nzeru konse, kodi mungamubwezere zotere Chauta? Iye ndiye Atate anu ndi Mlengi wanu, ndiye adakupangani ndi kukusandutsani mtundu. Kumbukirani zakale, lingalirani zamakedzana ndithu, funsani atate anu, akuuzani zimene zidachitika. Funsani akuluakulu, akufotokozerani zakalezo. Pamene Wopambanazonse adapereka maiko kwa anthu a mitundu ina, pamene adalekanitsa anthu, adaŵaikira malire potsata kuchuluka kwa anthu a Mulungu. Pajatu chigawo cha Chauta ndicho anthu ake, zidzukulu za Yakobe ndizo chigawo chakechake. Adaŵapeza m'chipululu, kuthengo kwenikweni kopanda kanthu. Adaŵatchinjiriza, ndipo adaŵasamala, monga momwe akadasamalira diso lake. Adachita ngati mphungu imene ikuphunzitsa ana ake kuuluka, imene ikungozungulira pamwamba pa ana akewo nitambalitsa mapiko ake, kuti igwire anawo ndi kuŵanyamula pa mapiko ake otambalitsa. Chauta yekha ndiye adatsogolera anthu ake, popanda thandizo la milungu yachilendo. Adaŵathandiza kuti azilamula maiko amapiri, ndipo adadya zomera zam'minda. Adaŵadyetsa uchi wam'mathanthwe, ndi mafuta ochokera m'nthaka yamiyala. Adaŵamwetsa chambiko wochokera ku ng'ombe ndiponso mkaka wankhosa, adaŵadyetsa nkhosa ndi mbuzi zonenepa, ndiponso nkhosa zamphongo zabwino za ku Basani, pamodzi ndi tirigu wabwino ndi vinyo wokoma. Yesuluni, anthu ake a Chauta adakulupala, koma iwowo adamuukira, adanenepa ndi kukula thupi, ndipo adakhuta zedi, kenaka adasiya Mulungu Mlengi wao, nanyoza mtetezi ndi mpulumutsi wao. Adamchititsa nsanje ndi mafano ao achilendo, ndipo zonyansa zimene adachita zidamkwiyitsa. Iwo adapereka nsembe kwa mizimu yoipa, imene siili milungu konse, milungu imene Aisraele sadaidziŵe nkale lonse, milungu yongobwera kumene, milungu imene makolo ao sankailemekeza konse. Adakana mtetezi wao amene adaŵalenga, adaiŵala Mulungu amene adaŵapatsa moyo. Chauta ataona zimenezi, adaŵakana anthuwo, chifukwa ana ao aamuna ndi aakazi adaautsa mkwiyo wake. Iye adati, “Ndidzaŵafulatira, ndidzaona chomwe chidzaŵachitikire, chifukwa anthu ameneŵa ngonyenga, ndi ana osakhulupirika. Milungu yao yabodza ndachita nayo nsanje, mafano ao andikwiyitsa nawo. Inenso ndidzaŵachititsa nsanje pakusamalira mtundu wina wachabechabe, ndipo ndidzaŵapsetsa mtima pakukondera fuko lina lopanda pake. Mkwiyo wanga udzayaka ngati moto, udzafika mpaka ku dziko la anthu akufa. Udzatentha zonse pa dziko, udzapsereza ndi mapiri omwe mpaka m'tsinde mwake. Ndidzaŵaunjikira masoka osatha, mipaliro yanga yonse idzathera pa iwowo. Ndidzaŵatumizira njala yoopsa, malungo ndi nthenda zofa nazo. Ndidzaŵatumizira zilombo zakuthengo zoŵavuta, zokwaŵa zaululu zidzaŵaluma. M'miseu adzafa chifukwa cha nkhondo, m'nyumba adzafa ndi mantha. Anyamata ndi atsikana adzafa, ngakhale ana ndi okalamba omwe sadzakhala ndi moyo. Achikhala ndidangoŵaononga kotheratu onsewo, kuti anthu pansi pano asaŵakumbukire ndi mmodzi yemwe! Koma sindifuna kuti adani ao azikandinyadira, sindifuna kuti adani azikaganiza molakwa, namanena kuti, ‘Tagonjetsa anthuwo ndife, si Mulungu amene adachita zonsezi.’ ” Aisraele ndi mtundu wopanda maganizo, alibe ndi nzeru zomwe. Achikhala anzeru, akadamvetsa, ndipo akadazindikira zimene zitha kudzaŵagwera. Nanga chifukwa chiyani munthu mmodzi adagonjetsa anthu chikwi chimodzi, ndipo anthu aŵiri adagonjetsa zikwi khumi? Nchifukwa chakuti Chauta, Mulungu wao, waŵasiya, Mulungu wao wamphamvu waŵataya. Adani ao amadziŵa kuti milungu yao ndi yopanda mphamvu, ndi yosalingana ndi Mulungu wa Aisraele. Adani ao ndi oipitsitsa ngati Sodomu ndi Gomora, Ali ngati mipesa yobala mphesa zoŵaŵa ndi zaululu, ndi oipa kwambiri ngati vinyo wosanganiza ndi ululu wa njoka, ululu wopweteka wa mphiri. Zimenezitu ndazisunga, ndi zobisika m'chikatikati cha mumtima mwanga. Kulipsira nkwanga, kubwezera zoyenerera nkwanganso, nthaŵi yoti agwe idzakwana. Tsiku la masoka ao layandikira, chiwonongeko chao chikudza mofulumira. Chauta adzachitira anthu ake zolungama, adzachitira atumiki ake zachifundo, pamene adzaona kuti mphamvu zao zatha, ndipo kuti sipatsala anthu, kaya ndi akapolo kapena mfulu. Pamenepo Chauta adzafunsa anthu ake kuti, “Nanga milungu yamphamvu yomwe mumaikhulupirira ija ili kuti? Mudaidyetsa mafuta a nsembe zanu, mudaipatsa vinyo woti imwe. Ibweretu kuti ikuthandizeni, ikutetezeni. Muwone tsopano kuti Mulungu uja ndine, Ine ndekha, palibenso mulungu wina. Ndimapha, Ine ndemwe ndimapatsanso moyo, ndimapweteka, Ine ndemwe ndimachiritsanso, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene angathe kupulumutsa munthu m'manja mwanga. Ndikukweza dzanja kumwamba, ndikulumbira pali Ine ndemwe wa moyo wosatha, kuti ndidzanola lupanga langa lochezimira, ndipo ndidzaona kuti chilungamo chichitike. Adani anga ndidzaŵabwezera chilango, amene amadana nane ndidzaŵalanga. Mivi yanga idzafiira ndi magazi ao ndipo lupanga langa lidzabayadi mnofu wao. Olasidwa ndi ogwidwa ukapolo magazi ao adzafalikadi, ndiponso mitu yao ya tsitsi litalilitali idzadulidwa.” Inu mitundu yonse ya anthu, tamandani anthu a Chauta. Chauta amalanga onse opha anthu ake, amalipsira adani ake, ndipo amachotsa tchimo m'dziko la anthu ake. Mose ndi Yoswa mwana wa Nuni adanena pamtima mau onse a nyimbo imeneyi, ndipo Aisraele ankamva. Mose atatha kuphunzitsa anthu mau onseŵa, adati: Mukumbukire bwino malamulo onse amene ndakupatsani leroŵa. Muuze ana anu kuti azimvera mosamala mau onse a malamuloŵa. Mauŵa sikuti ndi mau achabe. Mau ameneŵa ndiwo moyo wanu. Muŵamvere, ndipo mudzakhalitsa m'dziko mukukakhalamolo uko kutsidya kwa Yordani. Tsiku lomwelo, Chauta adalankhula ndi Mose kuti, “Kwera phiri loti Nebo ku mtandadza wa mapiri a Abarimu, umene uli m'dziko la Mowabu, kuyang'anana ndi mzinda wa Yeriko. Ulipenye dziko la Kanani limene ndikuŵapatsa Aisraele. Iwe udzafera pa phiri limenelo, monga mbale wako Aroni adafera pa phiri la Horo. Chifukwa chake nchakuti inu nonse aŵiri simudakhulupirike kwa Ine pamaso pa Aisraele. Pamene munali ku madzi a Meriba, pafupi ndi mudzi wa Kadesi, m'chipululu cha Zini, simudandilemekeze kokwanira pamaso pa Aisraele. Nchifukwa chake dziko limene ndikupatsa Aisraele uliwonere chapatali, koma kuloŵa kokha ndiye ai, suloŵamo”. Mose, munthu wa Mulungu uja, asanafe, adapereka madalitso kwa Aisraele. Poŵadalitsapo adanena mau akuti, “Chauta adabwera kuchokera ku phiri la Sinai, natitulukira kuchokera ku Seiri, ndipo adatiŵalira kuchokera ku phiri la Parani. Angelo zikwi khumi anali naye pamodzi, moto woyaka unali m'manja mwake. Chauta amakonda anthu ake ndipo amatchinjiriza onse amene ali opatulikira Iye. Anthuwo amaphunzira kwa Chauta, amamvera malangizo ake, ndiye kuti malamulo amene adatipatsa Mose. Malamulowo ndi chuma chopambana cha mtundu wa Yakobe. Chauta adakhala mfumu ya anthu ake Aisraele, pamene mafuko ao ndi atsogoleri ao adasonkhanitsidwa pamodzi.” Ponena za fuko la Rubeni, Mose adati, “Rubeni asafafanizike, akhalitse ndithu, ngakhale anthu ake ali pang'ono.” Za fuko la Yuda, adati, “Inu Chauta, mverani pamene iwo akulira, athandizeni, ndipo muŵalumikizenso ndi mafuko ena. Inu Chauta, muŵalimbikitse kuti adziteteze okha, ndipo muŵathandize polimbana ndi adani ao.” Za fuko la Levi adati, “Inu Chauta, Tumimu ndi Urimu adziŵitse kufuna kwanu kudzera mwa Alevi, atumiki anu okhulupirika. Mudaŵayesa ku Masa kuja, ndipo mudalimbana nawo ku madzi a Meriba kuja. Iwo adaonetsa kuti ankakhulupirira Inu kupambana makolo ao, abale ao kapenanso ana ao. Adamvera malamulo anu, ndipo adakhulupirika pa chipangano chanu. Iwowo ndiwo adzaphunzitse ana a Yakobe malangizo anu ndi Aisraele malamulo anu. Adzafukiza lubani pamaso panu, adzapereka nsembe zathunthu zopsereza pa guwa lanu. Inu Chauta, thandizani fuko lao kuti likhale lamphamvu, zochita zao zikukondwetseni. Otsutsana nawo ndi odana nawo onse muŵaononge, kotero kuti asadzadzukenso.” Za fuko la Benjamini adati, “Fuko ili ndilo limene Chauta amalikonda, ndipo amalitchinjiriza. Tsiku ndi tsiku Chauta amalisunga, pokhala m'kati mwa dziko laolo.” Za fuko la Yosefe adati, “Chauta adalitse dziko lao, likhale la mvula yambiri, ndipo la zitsime zochuluka. Dziko lao lidalitsidwe pokhala ndi zipatso zopsa ndi dzuŵa, likhalenso ndi zokolola zochuluka pa nyengo iliyonse. Mapiri ao akalekaleŵa akutidwe ndi zipatso, ndipo adzazidwe ndi zokolola zochuluka. Dziko lao likhale ndi dzinthu dzopambana, lidalitsidwe ndi zokoma za Chauta amene adalankhula m'chitsamba choyaka chija. Madalitso onseŵa atsikire fuko la Yosefe, popeza kuti anali mtsogoleri pakati pa abale ake. Yosefe ali ndi mphamvu zonga za ng'ombe yamphongo, nyanga zake ndi zonga za njati, adzapirikitsa anthu a mitundu ina ndi nyanga zimenezi. Onsewo adzaŵapirikitsira ku malekezero a dziko. Nyanga zimenezi ndi anthu zikwi khumi za Efuremu ndipo anthu zikwi za Manase.” Za mafuko a Zebuloni ndi Isakara, adati, “Zebuloni akondwere pa malonda ake, Isakara akondwere m'zithando mwake. Ku mapiri ao amaitanirako mitundu ya anthu, kumeneko amaperekako nsembe zoyenera, chifukwa choti amapeza chuma pochita malonda m'nyanja, kuchokera mu mchenga wa m'mbali mwa nyanja.” Za fuko la Gadi, adati, “Alemekezeke Chauta amene adakulitsa dziko la Gadi. Gadi amalalira ngati mkango waukazi, amamwetula dzanja ndi bade la mutu lomwe. Adadzitengera dziko labwino kuti likhale lao, gawo la mtsogoleri lidaperekedwa kwa iwowo. Adasunga maweruzo ndi malamulo a Chauta pamene atsogoleri a Aisraele adasonkhanitsidwa pamodzi.” Za fuko la Dani adati, “Dani ali ngati mwana wamkango, amene amalumpha kuchokera ku Basani.” Za fuko la Nafutali, adati, “Chauta wakomera mtima Nafutali namdalitsa kwambiri. Dziko lake lifika mpaka kumwera kuchokera ku nyanja ya Galileya.” Za fuko la Asere, adati, “Asere ndi wodalitsidwa kupambana mafuko ena. Abale ake amkonde, dziko lake likhale lachuma, la mitengo ya olivi. Midzi yake itchinjirizidwe ndi zitseko zachitsulo m'malinga, mphamvu zake zikhalitse monga masiku a moyo wake.” Inu Aisraele, palibe mulungu wina wofanafana ndi Mulungu wanu, amene amayenda ndi ulemerero mu mlengalenga, amakwera pa mitambo namabwera kudzakuthandizani. Chauta ndiye amene ali kothaŵirako ndipo pa dziko lapansili amakusungani ndi mphamvu zosatha. Adathaŵitsa adani anu onse pamene munkayenda, ndipo adakuuzani kuti muŵaononge onse. Motero Aisraele ali pa mtendere, zidzukulu za Yakobe zikusungidwa bwino m'dzikomo m'mene tirigu ndi vinyo sizisoŵa, m'mene mame amangogwa kuchokera kumwamba. Iwe Israele, ndiwetu wodala, wofanafana nawe palibe. Ndiwe mtundu umene Chauta adaupulumutsa. Chauta weniweniyo ndiye chishango chako ndi lupanga lako, ndiye amene amakutchinjiriza ndi kukupambanitsa. Adani ako adzafika kudzapempha kuti uŵachitire chifundo, koma iwe udzaŵapondereza pansi. Mose adakwera phiri la Nebo kuchokera ku zigwa za Mowabu. Adakafika mpaka pamwamba pa phiri la Pisiga kuvuma kwa Yeriko. Ndipo kumeneko Chauta adamuwonetsa dziko lonse, dziko la Giliyadi mpaka ku dziko la Dani. Dziko lonse la Nafutali, maiko onse a Efuremu ndi Manase, ndi dziko la Yuda mpaka kukafika ku Nyanja Yaikulu. Adamuwonetsanso chigawo chakumwera cha Negebu, ndi chigwa chimene chimafika mpaka ku Yeriko, mzinda wa mitengo ya migwalangwa, mpaka ku Zowari. Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Ilo ndilo dziko limene lija ndidalonjeza Abrahamu, Isaki ndi Yakobe, kuti ndidzapatsa zidzukulu zao. Ndakulola kuti uliwone, koma kuloŵamo kokha sindikulola.” Choncho Mose, mtumiki wa Chauta, adamwalira kumeneko m'dziko la Mowabu, monga momwe Chauta adanenera. Chauta adamuika ku Mowabu komweko m'chigwa, moyang'anana ndi mudzi wa Betepeori. Koma palibe ndi mmodzi yemwe amene akudziŵa malo enieni a mandawo. Mose adamwalira ali wa zaka 120. Koma anali wamphamvube, ndipo maso ake anali akuthwabe. Aisraele adalira maliro ake masiku makumi atatu m'chigwa cha Mowabu. Ndipo nthaŵi yolira maliro idatha. Tsono Yoswa, mwana wa Nuni, adadzazidwa ndi nzeru, chifukwa Mose adaamsanjika manja kuti aloŵe m'malo mwake. Aisraele adamvera Yoswa, ndi kutsata malamulo onse amene Chauta adaŵapatsa kudzera mwa Mose. Kuyambira pamenepo, sadakhaleponso mneneri wina aliyense wonga Mose. Chauta ankalankhula naye pamasompamaso. Palibe mneneri wina aliyense amene adachitapo zozizwitsa ndi zodabwitsa monga zimene Chauta adauza Mose kuti achite pamaso pa mfumu ya ku Ejipito, ndi pa akulu ake, ndi m'dziko lake lonse. Palibe mneneri wina aliyense amene adachita zinthu zazikulu ndi zoopsa zonga zimene adachita Mose pamaso pa Aisraele onse. Mose, mtumiki wa Chauta, atamwalira, Chauta adalankhula ndi mthandizi wake wa Moseyo, dzina lake Yoswa, mwana wa Nuni, kuti, “Mose, mtumiki wanga, wafa. Tsono iwe, konzeka tsopano pamodzi ndi Aisraele onseŵa, muwoloke mtsinje wa Yordaniwu, ndipo muloŵe m'dziko limene ndikuŵapatsalo. Paliponse pamene muponde phazi lanu, ndakupatsani inu, monga momwe ndidalonjezera Mose. Kuyambira ku chipululu kumwera, mpaka ku mapiri a Lebanoni kumpoto, kuchokeranso ku mtsinje waukulu wa Yufurate kuvuma, mpaka dziko lonse la Ahiti, kukafika ku Nyanja Yaikulu kuzambwe, lonseli lidzakhala dziko lanu. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzathe kukugonjetsa iwe Yoswa, nthaŵi yonse ya moyo wako. Ine ndidzakhala nawe monga momwe ndidakhalira ndi Mose, sindidzakusiya konse. Ukhale wamphamvu ndipo ulimbe mtima, chifukwa udzatsogolera anthu ameneŵa pokalandira dziko limene ndidalonjeza kwa makolo ao. Komatu ukhale wamphamvu ndipo ulimbe mtima kwambiri. Usamale ndithu kuti usunge malamulo onse amene Mose mtumiki wanga adakupatsa. Usatayepo ndi kagawo kamodzi komwe, ndipo kulikonse kumene udzapite, udzapambana. Uziŵerenga buku lamalamuloli, ndipo usana ndi usiku uzisinkhasinkha zolembedwa m'menemo, kuti uzisunge zonse. Tsono ukamatero, udzapeza bwino ndipo udzapambana. Paja ndidakulamula kuti ukhale wamphamvu. Usamaopa kapena kutaya mtima, poti Ine, Chauta, Mulungu wako, ndidzakhala nawe kulikonse kumene udzapite.” Pamenepo Yoswa adalamula atsogoleri a Aisraele naŵauza kuti, “Pitani ku zithando zonse, mukauze anthu kuti, ‘Konzekani, mangani katundu, chifukwa atapita masiku atatu, mudzaoloka Yordani ndi kulandira dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsani.’ ” Ndipo Yoswa adauza fuko la Rubeni ndi la Gadi ndi theka la fuko la Manase kuti, “Kumbukirani zija zimene Mose, mtumiki wa Chauta, adakuuzani, kuti, ‘Chauta, Mulungu wanu, adzakupatsani dziko limeneli kuti likhale lanu.’ Tsono akazi anu pamodzi ndi ana anu atsalire m'dziko lino la kuvuma kwa Yordani limene Mose adakupatsani. Ng'ombe zanu zitsalenso, koma ankhondo okha pakati panupa ndiwo aoloke atatenga zida, apite kutsogolo kwa Aisraele anzanu kuti akaŵathandize. Ndipo iwowo akadzalandira dzikolo ndi kukhazikikamo, pamenepo ndiye inu mudzabwerere ndi kudzakhala m'dziko lanu limene adakupatsani Mose, mtumiki wa Chauta, konkuno kuvuma kwa Yordani.” Onsewo adayankha Yoswa kuti, “Zonse zimene mwatilamulazi tidzachita, ndipo kulikonse kumene mudzatitume, tidzapita. Tidzakumverani monga momwe tidamverera Mose. Chauta, Mulungu wanu, akhale nanu, monga momwe adakhalira ndi Mose! Aliyense wokangana ndi inu kapena wosamvera malamulo anu, adzaphedwa. Inu mukhale amphamvu, ndipo mulimbe mtima kwambiri.” Tsono Yoswa, mwana wa Nuni, adatuma anthu aŵiri okazonda mwachinsinsi kuchokera ku Sitimu, naŵalangiza kuti, “Pitani, mukalizonde dzikolo, makamaka mukazondenso mzinda wa Yeriko.” Motero adapita anthu ozondawo, nakafikira ku nyumba ya mkazi wina wadama dzina lake Rahabu. Kumeneko nkumene adagona. Mfumu ya mzinda wa Yerikowo idamva kuti, “Aisraele ena afika mumzinda muno usiku, kudzazonda dziko.” Pomwepo mfumuyo idatuma anthu kwa Rahabu kukamuuza kuti, “Anthu amene ali m'nyumba mwakowo abwera kudzazonda dziko lonseli, tsono atulutse.” Koma pamenepo mkaziyo nkuti ataŵatenga amuna aŵiriwo naŵabisa, motero adayankha kuti, “Zoonadi kunyumba kwanga kuno kudaabwera anthu ena, koma kumene ankachokera, sindikudziŵa. Kuno achoka ndi chisisira, chipata cha mzinda uno chili pafupi kutsekedwa. Sindidaŵafunse kumene akupita, koma mukaŵalondola, mungathe kuŵapeza.” Pamenepo nkuti ataŵakweza pa denga azondiwo, nkuŵabisa pansi pa mapesi padengapo. Atangochoka anthu otumidwa ndi mfumuwo kutuluka mumzindamo, chipata chidatsekedwa. Ndipo adapita ku mseu kukaŵafunafuna azondiwo, mpaka adakafika ku dooko la Yordani. Tsono azondiwo asanagone, Rahabu adakwera padengapo naŵauza kuti, “Ndikudziŵa kuti Chauta wakupatsani dziko lonseli, ndipo tonsefe tikuchita mantha, mitima yathu ili thithithi! Inde, tamva m'mene Chauta adaphwetsera Nyanja Yofiira inu mukufika, m'mene munkatuluka ku Ejipito. Tamvanso m'mene mudakanthira mafumu aŵiri a Aamori, Sihoni ndi Ogi, kuvuma kwa Yordani kuja. Mudakantha ndi magulu ao ankhondo omwe. Titangomva zimenezi, tonsefe tidataya mtima, ndipo mantha adatigwira kukuwopani inu. Tikudziŵa kuti Chauta, Mulungu wanu, ndiye Mulungu wa kumwamba ndi dziko lonse lapansi. Tsopano mulumbire pamaso pa Chauta kuti mudzasunga zimene mulonjeze, ndipo kuti mudzachitira chifundo banja langa, monga momwe ndakusamalirani inu, ndipo munditsimikizire kwenikweni. Bambo wanga, mai wanga, pamodzi ndi alongo anga, abale anga ndi mabanja ao omwe, tonsefe mudzatisungire moyo, musadzatiphe.” Anthuwo adamuyankha kuti, “Ife tili okonzeka kufa kuti tikupulumutse iwe. Ukapanda kuulula zimene tachitazi, ifenso tidzasunga lonjezo lathu ndi iwe mokhulupirika, Chauta akadzatipatsa dzikoli.” Nyumba ya Rahabuyo idaali pa linga la mzindawo. Motero azondiwo atatulukira pa windo, Rahabu adaŵatsitsa pansi ndi chingwe. Anali ataŵauza kuti, “Pitani mudzere kumapiriko, kuti otumidwa ndi mfumu aja angakupezeni. Papite masiku atatu mukubisalabe, mpaka iwowo atachokako. Zitatero tsono, mungathe kumapita.” Tsono anthuwo adauza Rahabuyo kuti, “Lonjezo limene watilonjezetsali, tidzalisunga. Mvetsa tsono. Tikadzaloŵa, iweyo udzamange chingwe chofiirachi pawindo pomwe watitulutsirapa. Bambo wako, mai wako, abale ako ndi onse a m'banja la bambo wako, adzakhale m'nyumba mwako muno. Wina akadzatuluka m'nyumbamo kuti azidzayenda mu mseu, izo adzaone nzake, ife sitidzapalamula kanthu. Koma wina aliyense wokhala m'nyumba mwakomo akadzaona tsoka, mlandu udzakhala wathu. Komanso, ukangoulula zimene tikuchitazi, ife sitidzasunga lonjezo lathu tachitali.” Apo Rahabu adaŵayankha kuti, “Zikhaledi monga momwe mwaneneramo.” Pomwepo adaŵatulutsa, ndipo azondiwo adachoka. Tsono Rahabu adamanga chingwe chofiira pawindo paja. Pambuyo pake azondi aja adapita ku mapiri nakabisala, ndipo otumidwa ndi mfumu aja adaŵafunafuna ponseponse masiku atatu. Komabe sadapeze ndi mmodzi yemwe, motero adangobwerera. Pomwepo azondi aŵiri aja adatsika kumapiri kuja, ndipo ataoloka mtsinje uja, adakafika kwa Yoswa, namusimbira zimene adakumana nazo. Adauza Yoswayo kuti, “Ife tatsimikizadi kuti Chauta watipatsa dziko lonselo. Anthu onse kumeneko akuchita nafe mantha kwambiri.” M'mamaŵa kutacha Yoswa adanyamuka. Iye, pamodzi ndi Aisraele onse, adatuluka ku Sitimu kuja, napita ku Yordani, ndipo adagona kumeneko. Patapita masiku atatu, atsogoleri adakayendera zithando zonse, namauza anthu kuti, “Mukadzaona ansembe Achilevi aja atanyamula Bokosi lachipangano la Chauta, Mulungu wanu, mudzanyamuke pamalo panu ndi kuŵatsata. Potero mudzaidziŵa njira yoyenera kutsata, popeza kuti nkale lomwe kumeneko simudadzereko. Komatu tsono Bokosi lachipanganolo musaliyandikire. Pakati pa inu ndi Bokosilo pazikhala mtunda wosachepera kilomita imodzi.” Motero Yoswa adauza anthu onse kuti, “Mudzisungetu tsono, chifukwa maŵa Chauta adzachita zodabwitsa zazikulu pakati panu.” M'maŵa mwake Yoswa adauza ansembe kuti, “Nyamulani Bokosi lachipangano la Chauta, muwoloke, mutsogolere anthuwo.” Iwowo adachitadi monga momwe Yoswa adanenera. Apo Chauta adauza Yoswa kuti, “Zimene ndikuchita lerozi, ndizo zidzapatse Aisraele onse mtima wokulemekeza iwe, kuti ndiwe munthu wamkulu. Ndipo adzadziŵa kuti Ine ndili nawe monga momwe ndidakhalira ndi Mose. Ansembe amene akunyamula Bokosi lachipangano la Chauta, uŵalamule kuti, ‘Mukafika ku mtsinje wa Yordani, muloŵe m'madzimo ndi kuima m'mphepete.’ ” Tsono Yoswa adaŵauza anthuwo kuti, “Bwerani kuno, mudzamve zimene Chauta, Mulungu wanu, akukuuzani. Motero mudzadziŵa kuti Mulungu wamoyo ali pakati panu. Inu mukamapita patsogolo, Iye adzapirikitsa Akanani onse, pamodzi ndi Ahiti, Ahivi, Aperizi, Agirigasi, Aamori ndi Ayebusi. Pamenepo Bokosi lachipangano la Chauta wa dziko lonse lapansi liwoloke Yordani patsogolo panu. Tsopano musankhe amuna khumi ndi aŵiri kuchokera ku fuko lililonse la Aisraele. Ansembe onyamula Bokosi lachipangano la Chauta, Ambuye a dziko lonse lapansi, akangoponda madziwo, madzi onse a Yordani ochokera kumtunda adzaleka kuyenda, ndipo adzaima ngati chipupa.” Nyengo imeneyo inali ya kholola, ndipo mtsinje unali wodzaza kwambiri. Anthu onse adachoka ku zithando kukaoloka mtsinje wa Yordani uja. Ansembe ndiwo anali patsogolo, atanyamula Bokosi lachipangano la Chauta lija. Pamene ansembewo adafika pa chibumi cha Yordani, natsikira m'madzimo ndi kuponda madziwo, madzi onse adaima osayendanso. Madzi akumtunda adaundana ngati khoma lalitali, kuchokera ku Adama mpaka ku mzinda wa Zaretani. Madzi othamangira ku nyanja ya Araba, ndiye kuti Nyanja Yakufa, adatheratu pamalopo, ndipo anthu adaolokera tsidya lina, pafupi ndi Yeriko. Chonsecho nkuti ansembe onyamula Bokosi lachipangano la Chauta aja ataima pakatimpakati pa mtsinje wa Yordani uja, mpaka anthu onse adatha kuwoloka. Mtundu wonse wa Aisraele utaoloka Yordani, Chauta adauza Yoswa kuti, “Sankha amuna khumi ndi aŵiri, mmodzi pa fuko lililonse. Tsono uŵalamule kuti, ‘Tengani miyala khumi ndi iŵiri pakati penipeni pa mtsinje wa Yordanipo, pa malo amene anali kuimirira ansembewo. Nyamulani miyala imeneyo ndi kudza nayo ku zithando zanu kumene mudzagone usiku.’ ” Yoswa adaitana amuna khumi ndi aŵiri adaŵasankha aja, ndipo adaŵalamula kuti, “Loŵani mu mtsinje wa Yordaniwu patsogolo pa Bokosi lachipangano la Chauta, Mulungu wanu. Aliyense mwa inu atenge mwala pa phewa. Fuko lililonse la Aisraele litenge mwala umodzi. Miyala imeneyi idzakhala chikumbutso, ndipo anthu azidzakumbukira zimene Chauta wachita. Ana anu akamadzakufunsani m'tsogolo muno tanthauzo lake la miyala imeneyi, muzidzaŵauza kuti, ‘Madzi a Yordani adaaima osayendanso, pamene Bokosi lachipangano la Chauta linkaoloka mtsinjewu.’ Miyala imeneyi idzakhala chikumbutso kwa Aisraele.” Anthuwo adachitadi zonse zimene Yoswa adaŵalamula. Adanyamula miyala khumi ndi iŵiri pakati pa mtsinje wa Yordani, monga momwe Chauta adalamulira Yoswa. Anthu a fuko lililonse la Aisraele adanyamula mwala umodzi. Miyalayo adapita nayo kukaikhazika pansi pamalo pamene panali zithando paja. Yoswa adaimiritsa miyala khumi ndi iŵiri imene idaali pakati pa mtsinje wa Yordani, pamalo pomwe padaaimirira ansembe onyamula Bokosi lachipangano la Chauta aja. Miyala imeneyi ikadali kumeneko mpaka lero lino. Ansembe aja adaimirirabe pakati pa mtsinje wa Yordani, mpaka zitatha zonse zimene Chauta adaalamula Yoswa kuti auze anthu. Zimenezi ndizo zimene Mose anali atafotokozera Yoswa. Tsono anthu adaoloka mtsinjewo mofulumira. Ansembe atanyamula Bokosi lachipangano la Chauta adatsogolera anthu onse aja. Anthu a fuko la Rubeni ndi la Gadi ndi theka la Manase, ndiwo adaoloka poyamba, ali okonzekera nkhondo, monga momwe Mose adaŵauzira. Asilikali ngati zikwi makumi anai adaoloka, nakaima pa tsidya, m'chigwa cha Yeriko, ali okonzekera nkhondo. Zimene adachita Chauta pa tsiku limenelo zidapatsa anthu mtima wolemekeza Yoswa. Ndipo adamchitira ulemu kwambiri ndi kumlemekeza monga momwe ankalemekezera Mose nthaŵi yonse ya moyo wake. Onse ataoloka, Chauta adauza Yoswa kuti, “Lamula ansembe onyamula Bokosi lachipanganowo, kuti atuluke m'madzimo.” Yoswa adaŵalamuladi kuti atuluke. Ansembewo atangoponda pa mtunda, mtsinjewo udayamba kuyendanso mpaka kumasefukira m'chibumi. Aisraele adaoloka mtsinje wa Yordani tsiku lakhumi la mwezi woyamba, ndipo adamanga zithando zao ku Giligala, kuvuma kwa Yeriko. Kumeneko ndiko kumene Yoswa adaimiritsa miyala khumi ndi iŵiri ija imene adaaitenga ku Yordani. Ndipo adauza Aisraele onse aja kuti, “Ana akamadzafunsa makolo ao m'tsogolo muno kuti, ‘Kodi miyala imeneyi imatanthauzanji?’ Inuyo muzidzaŵauza kuti, ‘Aisraele adaoloka mtsinje wa Yordaniwu pansi pali pouma.’ Chauta, Mulungu wanu, ndiye adaaphwetsa madzi a mtsinjewo, kuti inuyo muwoloke pouma monga momwe adaaumitsira Nyanja Yofiira, mpaka tonse titaoloka. Chifukwa cha chimenechi, aliyense pa dziko lapansi pano adzadziŵa mphamvu za Chauta, ndipo mudzalemekeza Chauta, Mulungu wanu, mpaka muyaya.” Mafumu onse a Aamori amene ankakhala kuzambwe kwa Yordani, pamodzi ndi mafumu a Akanani okhala m'mphepete mwa nyanja, adamva kuti Chauta adaumitsa Yordani pamene Aisraele ankaoloka. Choncho adachita mantha, ndi kutayiratu mtima chifukwa cha Aisraelewo. Tsono Chauta adauza Yoswa kuti, “Sema miyala ngati mipeni, kuti uumbalire Aisraeleŵa.” Yoswa adasemadi mipeni yamiyalayo, naŵaumbala onsewo ku phiri lotchedwa “Koumbalira.” Adachita zimenezi chifukwa amuna amene anali oyenera kuponya nkhondo onse adaatha nkufa m'chipululu atatuluka ku Ejipito kuja. Anthu onse amene adaatuluka ku Ejipito anali ataumbalidwa kale, koma onse obadwira m'chipululu pa nthaŵi ya ulendo wofuma ku Ejipito anali osaumbalidwa. Aisraele adakhala akuyenda m'chipululu zaka makumi anai, mpaka adafa amuna onse amene potuluka ku Ejipito anali a msinkhu woyenera pa nkhondo. Adatha nkufa, popeza kuti sadamvere Chauta. Iye adaachita kuŵalumbirira kuti sadzaloŵamo m'dziko lamwanaalirenji lija limene adaalonjeza kwa makolo ao kuti adzaŵapatsa. Koma ana ao amene adaloŵa m'malo mwao, sadaumbalidwe pamene anali paulendo m'chipululumo, ndipo ndiwo amene Yoswa adalamula kuti aumbalidwe. Kuumbalako kutatha, Aisraele onse ankangokhala m'zithandomo kudikira kuti zilonda zipole. Tsono Chauta adauza Yoswa kuti, “Lero ndakuchotserani manyazi a ukapolo wanu uja umene munali nawo ku Ejipito.” Nchifukwa chake malowo adaŵatcha Giligala, ndipo mpaka lero lino malo ameneŵa akudziŵika ndi dzina limeneli. Pamene Aisraele anali m'zithando ku Giligala m'chigwa cha ku Yeriko, adachita Paska madzulo pa tsiku la 14 la mwezi woyamba womwewo. M'maŵa mwake mpamene anthu aja adayamba kudya chakudya cha ku Kanani. Adakazinga tirigu, naphikanso buledi wosatupitsa tsiku limenelo. Zitangotero, mana uja adaleka kugwa, ndipo sadapezekenso pakati pa Aisraele. Kuyambira nthaŵi imeneyo adayamba kudya chakudya cha ku Kanani. Tsiku lina pamene Yoswa anali pafupi ndi Yeriko, mwadzidzidzi adaona munthu ataimirira kutsogolo kwake, lupanga losolola lili m'manja. Tsono Yoswa adapita pomwe panali munthupo, namufunsa kuti, “Kodi iwe ndiwe mmodzi wa ankhondo athu kapena ndiwe mdani wathu?” Munthu uja adayankha kuti, “Sindine mmodzi mwa ankhondo anu kapenanso mdani wanu. Ndine mtsogoleri wa gulu lankhondo la Chauta pano.” Choncho Yoswa adadzigwetsa pansi chafufumimba naati, “Ine ndine wantchito wanu, mbuyanga. Nanga mufuna kuti ndichite chiyani?” Wolamula gulu lankhondo la Chauta uja adamuyankha kuti, “Vula nsapato zako. Malo amene ukuimirirapoŵa ngoyera.” Yoswa adachitadi zimene adamuuzazo. Mzinda wa Yeriko udaali utatsekedwa pa zipata zake zonse, kuti Aisraele asaloŵe. Panalibe ndi mmodzi yemwe wotuluka kapena kuloŵa mumzindamo. Chauta adauza Yoswa kuti, “Mvetsa! Yeriko, pamodzi ndi mfumu yake ndi ankhondo ake amphamvu, ndakupatsa iwe. Iwe pamodzi ndi ankhondo, muzizungulira mzinda umenewu masiku asanu ndi limodzi, kamodzi pa tsiku. Ansembe asanu ndi aŵiri, aliyense lipenga la nyanga yankhosa lili kumanja, ndiwo azitsogolera Bokosi lachipangano. Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, iwe ndi ankhondowo, mudzazungulire mzinda umenewu kasanunkaŵiri, ansembe akuliza malipengawo. Tsono adzalize mosalekeza ndi mwamphamvu zedi. Ndipo anthu akadzangomva kuliza koteroko, adzafuule kolimba, motero makoma a mzindawo adzagwa. Apo ankhondo ako onse adzaloŵa mumzindamo.” Pomwepo Yoswa adaitana ansembe naŵauza kuti, “Nyamulani Bokosi lachipangano ndipo ansembe asanu ndi aŵiri mwa inu apite patsogolo pa Bokosilo atanyamula malipenga a nyanga zankhosa, koma ankhondo ndiwo akhale patsogolo.” Ndipo adauza anthu kuti, “Yambamponi. Yendani mozungulira mzindawo, ankhondo akhale patsogolo pa Bokosi lachipangano.” Tsono, potsata mau a Yoswa aja, ansembe asanu ndi aŵiri aja adapita patsogolo pa Bokosi lachipangano la Chauta, akuliza malipenga a nyanga zankhosa zija. Ndipo ankhondo ndiwo anali patsogolo pa ansembe. Ankhondo ena anali pambuyo, ankatsatira Bokosi lachipanganolo. M'menemo nkuti malipenga ali pakati kulira. Koma Yoswa adalamula anthu kuti asafuule kapena kuchita phokoso mpaka iye atalamula. Motero ansembe onyamula Bokosi lachipangano la Chauta aja, adazungulira mzindawo kamodzi. Atatero, iwo ndi ankhondo adabwerera ku zithando, nakagona. Yoswa adauka m'mamaŵa, ndipo ansembewo adanyamulanso Bokosi lachipangano la Chauta. Ansembe asanu ndi aŵiri onyamula malipenga a nyanga zankhosa aja, adatsogolako akulizanso malipengawo. Ankhondo anali patsogolo, ndipo gulu lina la ankhondo linali kutsata pambuyo pa Bokosilo. Pamenepo nkuti malipenga ali pakati kulira. Pa tsiku lachiŵiri adauzunguliranso mzindawo kamodzi, nabwerera ku zithando. Adachita zimenezi masiku asanu ndi limodzi. Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, adadzuka m'mbandakucha, ndipo adazungulira mzindawo kasanunkaŵiri. Ndi pa tsiku limenelo lokha pomwe adazungulira mzindawo kasanunkaŵiri. Kuzungulira kwakasanunkaŵiri kutatha, ansembe aja akuliza malipenga, Yoswa adauza anthu kuti, “Fuulani! Chauta wakupatsani mzindawu. Mzindawu pamodzi ndi zonse za m'menemu muwononge, kuti zikhale ngati nsembe zopereka kwa Chauta. Koma Rahabu yekha wadama uja ndi onse a m'nyumba mwake, muŵasunge poti ndiye adabisa azondi athu aja. Koma inu, musatenge kalikonse koyenera kuwonongedwa. Mukangotengako kalikonse koyenera kuwonongedwa, mudzaputa mavuto, ndipo zithando za Aisraele zidzaonongedwa. Koma zonse zasiliva ndi zagolide, ndiponso zipangizo zamkuŵa ndi zachitsulo zikhale zopatulika za Chauta.” Pomwepo ansembe adalizanso malipenga aja. Anthu atamva, adafuula kwambiri, ndipo linga la mzindawo lidagwa. Ndipo ankhondo onse adabwera nakaloŵa mu mzindawo, naulanda. Tsono adaloŵa mu mzinda, malupanga ali m'manja, napha onse ndi lupanga, kuyambira amuna, akazi, ana ndi nkhalamba zomwe. Adaphanso zoŵeta zonse, monga ng'ombe, nkhosa ndi abulu. Yoswa adauza anthu aŵiri amene adakazonda aja kuti, “Pitani ku nyumba ya mkazi wadamayo, ndipo iye pamodzi ndi onse a m'nyumba mwake abwere kuno, monga mudamlonjezera.” Iwo adapita, nakatenga Rahabu pamodzi ndi bambo wake, mai wake, abale ake, ndi onse a m'banja laolo. Adabwera nawo onse a m'banja laolo naŵaika kuseri kwa zithando za Aisraele. Atatero, mzinda wonsewo adauthira moto, pamodzi ndi zonse zimene zinali m'menemo, kupatula zagolide ndi zasiliva, ndiponso zipangizo zamkuŵa ndi za chitsulo, zimene adatenga nazisunga mosungira chuma cha Nyumba ya Chauta. Koma Yoswa adamsiya ali moyo Rahabu wadama uja, pamodzi ndi abale ake onse, poti ndiye adaabisa azondi aja amene Yoswayo adaaŵatuma kukazonda Yeriko. Zidzukulu zake za Rahabu zilipo pakati pa Aisraele mpaka lero lino. Pa nthaŵi imeneyo Yoswa adapereka chenjezo motemberera kuti, “Aliyense amene adzamangenso mzinda wa Yerikowu, Chauta adzamtemberere. Aliyense amene adzamange maziko ake, mwana wake wachisamba adzafa. Aliyense amene adzamange zipata zake, mzime wake adzafa.” Motero Chauta anali ndi Yoswa, ndipo mbiri yake idawanda m'dziko lonselo. Koma Aisraele ena sadamvere lamulo la Chauta loti asatenge kanthu kena kalikonse koyenera kuwonongedwa. Tsono amene adaagwinyako zinthuzo, anali Akani. Iyeyu anali mwana wa Karimi, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda. Choncho Chauta adakwiyira Aisraele onse kwambiri. Atagonjetsa Yeriko, Yoswa adatuma anthu ena kuti akazonde mzinda wa Ai. Mzinda umenewu unali kuvuma kwa Betele, pafupi ndi Betaveni. Ataŵatuma kuti akazonde mzindawo, anthu aja adapitadi nazonda mzinda wa Ai. Atabwerera kwa Yoswa, anthuwo adamuuza kuti, “Sikofunikira kuti tipite tonse kumeneko. Ingotumani anthu zikwi ziŵiri kapena zitatu kuti akathire nkhondo mzinda wa Ai. Musatume anthu onse kumeneko poti si mzinda waukulu.” Motero Yoswa adangotuma anthu ngati zikwi zitatu. Koma tsono anthu a ku Ai adapirikitsa Aisraelewo. Anthu a ku Ai adathamangitsa Aisraele kuchokera ku chipata cha mzindawo mpaka ku ngwenya. Aisraele okwanira ngati 36 adaphedwa, makamaka pamene ankatsika phiri. Motero Aisraele onse adataya mtima, ndipo adachita mantha kwambiri. Yoswa atamva zimenezi, adamva chisoni kwambiri, ndipo adang'amba zovala zake, nagwada patsogolo pa Bokosi lachipangano la Chauta lija. Atsogoleri onse a Aisraele nawonso adadzigwetsa pansi pa malo omwewo mpaka madzulo, atadzola fumbi kumutu, kusonyeza chisoni chaocho. Tsono Yoswa adati, “Kalanga ine Chauta! Chifukwa chiyani mudatiwolotsa Yordani? Kani mudatipereka m'manja mwa Aamori kuti atiwononge chotere? Bwanji osangotileka kuti tikhale tsidya ilo la Yordani? Nanga ndinene chiyani tsopano, Chauta, poona kuti Aisraele athamangitsidwa ndi adani ao chotero? Akanani ndi anthu ena onse okhala m'dziko muno adzamva zimenezi, ndipo adzatizinga ndi kutipha tonse. Kodi pamenepa inu mudzachitapo chiyani kuti ulemu wanu usaonongeke?” Chauta adamuuza Yoswa kuti, “Dzuka, chifukwa chiyani wagwada pansi chotere? Aisraele ena adachimwa. Chipangano chija ndidapangana nawochi sadasunge. Zinthu zija ndidaŵauza kuti aonongezi, adagwinyako. Adabako, ndi kunenanso bodza, namaika zinthu zakubazo pakati pa zinthu zao. Nchifukwa chake Aisraele sangathe kulimbana ndi adani ao. Athaŵa pamaso pa adani ao chifukwa choti iwowo ngoyenera kuwonongedwa. Sindidzakhala nawonso mpaka utaononga zinthu zimene ndidakulamula kuti usatenge. Nyamuka, ukalamule anthu kuti adzipatule, kuti akonzekere kuwonana ndi Ine maŵa, chifukwa Ine Mulungu wa Aisraele ndidzaŵauza kuti, ‘Inu Aisraele, zinthu zija ndidaakuuzani kuti muwonongezi, zili pakati panu. Inu simungalimbe polimbana ndi adani anu, mpaka zinthu zimenezi mutachotsa.’ Motero maŵa m'maŵa, mutulukire poyera nonsenu, fuko limodzilimodzi. Fuko limene Ine Chauta ndidzaliloze lidzabwera patsogolo, mbumba imodziimodzi. Mbumba imene ndidzailoze idzabwera patsogolo, banja limodzilimodzi. Banja limene ndidzaliloze lidzabwera patsogolo, munthu mmodzimmodzi Yemwe adzapezeke ndi zinthu zimenezo, adzatenthedwa pamodzi ndi banja lake lonse ndi zonse zomwe ali nazo. Chinthu chimene wachitacho nchoopsa, chifukwa waphwanya pangano lomwe anthu anga adachita ndi Ine.” M'maŵa mwake Yoswa adadzuka m'mamaŵa, natulutsa Aisraele onse fuko limodzilimodzi. Fuko la Yuda lidalozedwa. Mbumba zonse za fuko la Yuda adazitulutsira poyera, ndipo mbumba ya Zera idagwidwa. Tsono mabanja a Zera adaŵatulutsira poyera, ndipo banja la Zabidi lidagwidwa. Pompo Yoswa adatulutsa anthu onse a banja la Zabidi, ndipo Akani adagwidwa. Iyeyo anali mwana wa Karimi, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda. Tsono Yoswa adauza Akani kuti, “Iwe mwana wanga, lemekeza Chauta, Mulungu wa Aisraele, ndipo umtamande. Uze tsopano lino zimene wachita. Usati undibisire.” Akani adayankha kuti, “Indedi, ine ndidachimwa, ndidachimwira Chauta, Mulungu wa Aisraele, ndipo zimene ndidachita ndi izi: pakati pa chuma chija, ndidaonapo mwinjiro wokongola wa ku Babiloni, ndi makilogramu aŵiri a siliva ndiponso munsi wa golide wolemera theka la kilogramu. Zonsezi ndidaazikhumba kwambiri, kotero kuti ndidatenga ndithu. Mungathe kuzipeza m'chithando changa m'mene ndidazibisa. Mukapezanso silivayo pansi pa zinthu zinazo.” Motero Yoswa adatuma anthu ena kuti apite kuchithandoko, ndipo adakapezadi kuti zonsezo adazibisa kumeneko, ndipo kuti silivayo adamubisadi pansi. Adazitulutsa zonsezo m'chithandomo, napita nazo kwa Yoswa ndi kwa Aisraele onse. Ndipo adaziika pamaso pa Chauta. Yoswa ndi Aisraele onse adamtenga Akani ndi zinthu zimene adapezeka nazo zija monga silivayo, mwinjiro ndi munsi wa golide uja. Adatenganso ana ake aamuna ndi aakazi omwe, ndi zoŵeta zake, ng'ombe, abulu, nkhosa, ndi hema lake ndi zonse zomwe anali nazo. Zonsezo adapita nazo ku chigwa chotchedwa Akori. Tsono Yoswa adati, “Chifukwa chiyani watiputira mavuto otereŵa? Tsopano Chauta ndiye amene adzetse mavuto ameneŵa pa iwe!” Pompo anthu onsewo adamponya miyala Akani, namupha. Adaponya miyala banja lake lonse, mpakanso kulitentha pamodzi ndi zake zonse. Adaunjika mulu waukulu wamiyala pa iyeyo, ndipo muluwo ulipo mpaka lero lino. Nchifukwa chake mpaka lero chigwa chimenechi amachitchula kuti “Chigwa cha Mavuto.” Motero mtima wa Chauta udatsika. Pambuyo pake Chauta adauza Yoswa kuti, “Usachite mantha kapena kutaya mtima. Tenga ankhondo onse, ndipo upite nawo ku Ai. Ndidzapereka m'manja mwanu mfumu ya ku Ai pamodzi ndi anthu ake onse. Mzindawo pamodzi ndi dzikolo, zonsezo zidzakhala zanu. Mzinda wa Ai ndi mfumu yake yomwe, muuchite zomwe mudachita Yeriko ndi mfumu yake. Koma katundu wamumzindamo ndi zoŵeta, musunge zikhale zanu. Muulalire mzindawo, ndipo muuthire nkhondo cha kumbuyo kwake.” Motero Yoswa adakonzeka ndi ankhondo ake kupita ku Ai. Adasankhula ankhondo ena olimba mtima zikwi makumi atatu, ndipo adaŵatuma usiku. Adaŵapatsa malamulo akuti, “Kabisaleni kumbuyo kwa mzindawo. Musakapite patali ndi mzindawo, koma kakhaleni okonzekera kuuthira nkhondo. Anthu anga pamodzi ndi ine ndiye tidzayambe kuuputa mzindawo cha kumaso kwake. Tsono akadzangotuluka kuti alimbane nafe, ife tidzabwerera m'mbuyo, monga momwe tidachitira tsiku lina lija. Adzatithamangitsa motero, mpaka ife titaona kuti ali kutali ndi mzindawo, chifukwa iwowo azidzati, ‘Akutithaŵa monga kale lija.’ Pamenepo tsono mudzatuluke kuja mudzakhale mutabisalaku, ndipo mudzalanda mzindawo. Chauta, Mulungu wanu, adzakupatsani mzinda umenewo. Mutaulanda, dzauyatseni moto, monga Chauta walamulira. Ameneŵa ndiwo malamulo amene ndakupatsani.” Motero Yoswa adaŵatuma, ndipo iwo adapita ku malo obisalakowo kukaulalira mzindawo. Malowo anali cha kuzambwe kwa Ai, pakati pa Ai ndi Betele. Koma Yoswa ndi gulu lake lankhondo adakhala m'zithando usiku wonse. M'mamaŵa, Yoswa adadzuka naitana ankhondo ake onse. Tsono iyeyo ndi atsogoleri a Aisraele, adapita ku Ai. Ankhondo omwe anali ndi iyeyo adatsogolako, nakamanga zithando chakumpoto kupenyana ndi chipata cha mzindawo. Pakati pa iwowo ndi mzinda wa Aiwo panali chigwa. Yoswa adapatula anthu zikwi zisanu, naŵabisa cha kuzambwe kwa mzindawo, pakati pa Ai ndi Betele. Adakhazika ankhondo mokonzekera nkhondo, ndipo gulu lalikulu la ankhondowo lidamanga zithando cha kumpoto kwa mzinda, m'chigwamo, koma gulu lina lija lidakamanga chakuzambwe. Mfumu ya ku Ai itaona anthu a Yoswawo, idachita zinthu mofulumira. Pamodzi ndi anthu ake idapita ku malo otsika oyang'anana ndi Araba, kuti ikamenyane ndi Aisraele kumeneko ngati kale lija. Iyo sinkadziŵa kuti aithira nkhondo cha kumbuyo kwake. Yoswa pamodzi ndi anthu akewo adachita ngati akuthaŵa, kumaloŵera chakuthengo ndithu. Anthu onse amumzindamo adauzidwa kuti aŵatsate pambuyo, ndipo pamene ankapirikitsa Yoswa, iyeyo ankathaŵira kutsogolo ndithu, kutalikirana ndi mzinda wao uja. Choncho mwamuna aliyense wamumzindamo anali atatulukamo kuthamangitsa Aisraele. Mzindawo udangotsala wokha, popanda woti angautchinjirize. Tsono Chauta adauza Yoswa kuti, “Loza mkondo wako ku Ai. Mzindawu ndikukupatsa iwe.” Yoswa adachitadi monga adamuuzira. Tsono atangokweza dzanja lake, anthu amene adabisala aja, adavumbuluka msangamsanga, adathamangira mu mzindawo naugonjetsa, ndipo adautentha pomwepo. Anthu a ku Ai aja atacheukira m'mbuyo adangoona utsi uli tolotolo! Malo oti iwowo athaŵireko panalibe, chifukwa choti Aisraele aja adaathaŵira kuthengoŵa adabwerera kudzalimbana nawo. Yoswa ndi anthu anali nawo aja, ataona kuti anzao aja alanda mzindawo, ndipo kuti utsi uli tolotolo, adatembenuka nayamba kupha anthu a ku Ai aja. Nawonso Aisraele amene anali mumzindamo adabwera kudzalimbana ndi anthu a ku Ai. Choncho onsewo anali atazingidwa ndi Aisraele, ndipo onsewo adaphedwa. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adapulumuka kapena kutulukamo wamoyo, koma mfumu ya ku Ai yokha. Mfumuyo adaigwira, napita nayo kwa Yoswa. Motero Aisraele adapha adani ao m'chigwa ndi m'thengo m'mene adaŵapirikitsira. Ndipo adabwereranso ku Ai, naphanso otsala amene anali kumeneko. Chiŵerengero chonse cha anthu a ku Ai amene adaphedwa pa tsikulo chinali zikwi khumi ndi ziŵiri, amuna ndi akazi omwe pamodzi. Yoswa ankalozabe mkondo wake uja ku Ai, osatsitsa dzanja lake mpaka munthu aliyense mumzindamo ataphedwa. Ndipo Aisraele adatenga zoŵeta ndi katundu yense wamumzindawo, monga momwe Chauta adauzira Yoswa. Pomwepo Yoswa adautentha mzinda wa Ai, nausiya bwinja monga uliri leromu. Mfumu ya mzindawo adaipachika pa mtengo ndi kuisiya pompo mpaka madzulo. Madzulo ndi kachisisira, Yoswa adalamula kuti akatsitse mtembowo, ndipo atatero adautaya pansi ku chipata cha mzindawo. Pamwamba pa mtembowo adaunjikapo mulu wa miyala. Muluwo uli pomwepo mpaka lero lino. Tsono Yoswa adamangira Chauta guwa pa phiri la Ebala. Adalimanga potsata malangizo amene Mose mtumiki wa Chauta adaapatsa Aisraele, ndi potsata mau a m'buku la malamulo a Mose onena kuti, “Guwa likhale la miyala yosasema ndi zipangizo zachitsulo.” Pa guwa limenelo adaperekapo nsembe zopsereza kwa Chauta, ndipo adaperekanso zopereka zamtendere. Kumeneko, Aisraele onse akupenya, Yoswa adalemba pa miyala chitsanzo cha malamulo aja amene Mose adaalemba. Aisraele onse, pamodzi ndi atsogoleri ao, akuluakulu ao, aweruzi ao ndiponso alendo omwe amene anali pakati pao, adaimirira pa mbali ziŵiri za Bokosi lachipangano lija, ena uku ena uku, moyang'anana ndi ansembe Achilevi amene anali kunyamula Bokosilo. Theka lina la anthu lidaimirira kuyang'anana ndi phiri la Gerizimu, ndipo theka lina kuyang'anana ndi phiri la Ebala. Pachiyambi penipeni, Mose mtumiki wa Chauta adaaŵalamula iwowo kuti azichita zimenezi pofuna kulandira madalitso. Tsono Yoswa adaŵerenga mau onse a malamulo momveka bwino, pamodzi ndi madalitso ndiponso matemberero, monga momwe zidalembedwera m'buku la malamulo a Mose. Yoswayo adaŵerenga lililonse mwa malamulo a Mose, kuŵerengera anthu onse amene adasonkhana. Akazi ndi ana, pamodzi ndi alendo omwe okhala pakati pao, anali pomwepo. Mafumu onse okhala kuzambwe kwa Yordani adamva zimenezi. Onse okhala ku mapiri, m'zigwa ndiponso m'mbali mwa Nyanja Yaikulu cha kumpoto kwa Lebanoni, nawonso adamva. Ameneŵa ndiwo mafumu a Ahiti, Aamori, Akanani, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi. Ndiye onseŵa adapangana za kulimbana ndi Yoswa ndi Aisraele onse. Tsono Ahivi a ku Gibiyoni atamva zimene Yoswa adaachita mzinda wa Yeriko ndi wa Ai, adaganiza zoti amugwire m'maso. Adapita nasenzetsa abulu chakudya cha m'matumba akalekale, ndiponso matumba a vinyo a chikopa cha zigamba zokhazokha. Adavala nsapato zothaitha za zigamba zokhazokha, ndiponso zovala zansanza. Buledi amene adatenga anali wouma ndi wachuku. Tsono adapita kwa Yoswa ku zithando ku Giligala kuja, namuuza iyeyo pamodzi ndi Aisraele onse kuti, “Ife tachoka ku dziko lakutali, ndipo tikufuna kuti tichite nanu chipangano.” Koma Aisraele adayankha kuti, “Mwina mwake kwanu nkufupi konkuno. Nanga tingachite nanu chipangano bwanji?” Iwo adauza Yoswa kuti, “Ife ndife akapolo anu.” Tsono Yoswa adaŵafunsa kuti, “Kodi inu ndinu yani? Mwachoka kuti?” Anthuwo adamuuza nkhani yonse, adati, “Ife tachoka kutali kwambiri, chifukwa choti tamva za Chauta, Mulungu wanu. Tamva mbiri yonse ya zimene Iye adachita ku Ejipito, ndiponso zimene adachita kwa mafumu aŵiri a Aamori kuvuma kwa Yordani, kwa Sihoni mfumu ya ku Hesiboni, ndiponso kwa Ogi, mfumu ya ku Basani, imene imakhala ku Asitaroti. Tsono atsogoleri athu ndi anthu onse okhala m'dziko lathu adatiwuza kuti, ‘Konzani chakudya chapaulendo, pitani mukakumane nawo anthu amenewo ndipo mukanene kuti, “Ife tadzagonja, chonde mupangane nafe zamtendere.” ’ Tangoonani bulediyu. Pochoka kwathu, buledi ameneyu anali wofunda ndithu, koma tangoonani ali gwaa ndiponso wochita chuku. Pamene tinali kuthira vinyo, matumbaŵa anali atsopano ndithu, koma taonani ngong'ambika. Zovala zathu ndi nsapatozi zangokhala nsanza zokhazokha, chifukwa cha kutalika kwa ulendo.” Ndipo Aisraele adalaŵako chakudya chao, osafunsa Chauta. Motero Yoswa adapangana nawo za mtendere, nanena kuti sadzaŵapha. Atsogoleri a Aisraelewo adatsimikiza chipanganocho ndi malumbiro. Patangopita masiku atatu atachita chipanganocho, Aisraele adaŵazindikira anthuwo kuti ngochokera pafupi. Tsono Aisraele adachoka napita kwao kwa anthuwo, napeza kuti mizinda yao inali Gibiyoni, Kefira, Beeroti ndi Kiriyati-Yearimu. Komatu Aisraele sadathe kuŵapha anthuwo, poti paja atsogoleri ao anali atalonjeza m'dzina la Chauta, Mulungu wa Israele, za anthu ameneŵa; apo Aisraele ena adayamba kudandaula kwa atsogoleri za zimenezi. Koma atsogoleriwo adayankha kuti, “Ife tidaŵalonjeza m'dzina la Chauta, Mulungu wa Aisraele, ndipo tsopano sitingathe kuŵapha. Tiŵalole akhale moyo, kuti ukali wa Mulungu ungatigwere. Alekeni akhale moyo, komatu azitidulira nkhuni ndi kumatitungiranso madzi.” Zimenezi ndizo zimene adanena atsogoleri aja. Yoswa adaŵaitana Agibiyoniwo, naŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mudatinyenga potiwuza kuti mwachokera kutali, chikhalirecho ndinu a pafupi pompano? Popeza kuti mwachita zimenezi, Mulungu wakutembererani. Nthaŵi zonse inu ndiye muzidzatidulira nkhuni, ndi kutitungira madzi ku Nyumba ya Mulungu.” Ndipo iwo adayankha kuti, “Mbuyathu, ife tidachita zimenezi chifukwa choti tidamva kuti Chauta, Mulungu wanu, adalamula mtumiki wake Mose kuti adzakupatseni dziko lonseli, ndipo kuti mudzaphe anthu onse kulikonse kumene mukaŵapeze. Motero tidachita zimenezi poti tidakuwopani kwambiri ndipo tidafuna kupulumutsa moyo wathu. Tsopano lino, otilamulira ndinu, ndipo mungotichita zimene zingakukomereni,” Apo Yoswa adaŵatchinjiriza anthuwo, kuti Aisraele angaŵachite zoipa, kapena kuŵapha. Komabe nthaŵi yomweyo, adasanduka odulira anthu nkhuni, ndiponso otunga madzi a ku guwa lansembe la Chauta. Mpakana lero lino, akuchitabe zimenezi ku malo aliwonse amene Chauta adasankha. Adonizedeki mfumu ya ku Yerusalemu adamva kuti Yoswa wagonjetsa kotheratu mzinda wa Ai, ndipo waononga mzindawo pamodzi ndi mfumu yake, monga momwe adachitira Yeriko pamodzi ndi mfumu yake yomwe. Adamvanso kuti anthu a ku Gibiyoni adapangana za mtendere ndi Aisraele, ndipo kuti anali kukhala pakati pao. Motero anthu a ku Yerusalemu adachita mantha kwambiri, pakuti Gibiyoni unali mzinda waukulu, monga mzinda uliwonse wokhala ndi mfumu. Unali waukulu kupambana Ai, ndipo ankhondo ake anali olimba mtima. Motero Adonizedeki adatuma mithenga kwa Hohamu mfumu ya ku Hebroni, kwa Piramu mfumu ya ku Yaramuti, kwa Yafiya mfumu ya ku Lakisi ndi kwa Debiri mfumu ya ku Egiloni. Adatuma mau akuti, “Bwerani mudzandithandize kumenyana ndi Gibiyoni, chifukwa anthu ake apangana za mtendere ndi Yoswa ndiponso ndi Aisraele onse.” Mafumu asanu a Aamoriwo, mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yaramuti, mfumu ya ku Lakisi ndiponso ya ku Egiloni, adagwirizana. Adasonkhanitsa ankhondo ao nazinga mzinda wa Gibiyoni, ndi kuuthira nkhondo. Anthu a ku Gibiyoni adatumiza mau kwa Yoswa ku zithando ku Giligala kuja kuti, “Mbuyathu, musatitaye ife atumiki anu. Bwerani msanga mudzatithandize! Tipulumutseni! Mafumu onse a Aamori atsika mapiri kudzamenyana nafe.” Tsono Yoswa ndi ankhondo ake onse ndi anthu ake onse olimba mtima adayambapo ulendo kuchoka ku Giligala. Ndipo Chauta adauza Yoswa kuti, “Usaŵaope anthu amenewo. Ndaŵapereka kale kwa iwe kuti uŵagonjetse. Palibe ndi mmodzi yemwe mwa iwo amene adzatha kulimbika.” Yoswa ndi ankhondo ake adayenda usiku wonse kuchoka ku Giligala, ndipo adakathira nkhondo mwadzidzidzi. Chauta adaŵachititsa mantha adaniwo pamene adangoona nkhondo ya Aisraele ija. Motero Aisraele adapambana Aamori ku Gibiyoni, naŵathamangitsa kutsika phiri la ku Betehoroni ndi kuŵakantha mpaka ku Azeka ndi ku Makeda. Pamene ankathaŵa nkhondo ya Aisraeleyo kutsika phiri ku Betehoroni mpaka ku Azeka, Chauta adagwetsa miyala yaikulu yamatalala pa iwo kuchokera kumwamba, ndipo idaŵapha. Ophedwa ndi matalala anali ambiri kupambana ophedwa ndi Aisraele. Pa tsiku limene Chauta adapatsa Aisraele mphamvu kuti agonjetse Aamori, Yoswa adalankhula naye. Tsono pamaso pa Aisraele onse adati, “Iwe dzuŵa, ima pamwamba pa Gibiyoni, iwe mwezi, ima pamwamba pa chigwa cha Ayaloni.” Choncho dzuŵa lidaima pamodzimodzi, ndipo mwezi sudayendenso mpaka Aisraele atagonjetsa adaniwo kotheratu. Zimenezi zidalembedwa m'buku la Yasara. Dzuŵa lidangoima pamodzimodzi pakati pa mutu mu mlengalenga, ndipo silidayendenso mofulumira pafupi tsiku lonse. Chiyambire nkale lonse, sipadaonekepo tsiku longa limeneli loti Chauta adamvera munthu, popeza kuti ankamenyera Israele nkhondo. Zitatha izo Yoswa ndi gulu lake lankhondo adabwerera ku zithando ku Giligala. Mafumu asanu onse aja adathaŵa nakabisala ku phanga ku Makeda. Pambuyo pake adapezeka, ndipo ena adadzauza Yoswa kuti mafumuwo akubisala kumeneko. Iye adalamula kuti, “Kunkhuniziranipo miyala pa khomo la phangalo, ndipo muikepo alonda. Koma inuyo musakhaleko kumeneko. Muŵapirikitse adaniwo, ndipo muŵathire nkhondo kuchokera kumbuyo. Musalole kuti akafike ku mizinda yao. Chauta, Mulungu wanu, wakupatsani mphamvu zoŵagonjetsera.” Ndipo Yoswa pamodzi ndi Aisraele adapha anthuwo. Amene sadaphedwe ndi okhawo amene adabisala m'mizinda yamalinga. Tsono anthu onse a Yoswa adabwerako bwino, nakafika ku zithando ku Makeda. Palibe ndi mmodzi yemwe m'dzikomo amene adayesanso kuputa Aisraele. Tsono Yoswa adati, “Tsekulani khomo la phanga lija, ndipo mafumu asanuwo mubwere nawo kuno.” Anthu adachita zimenezo: mafumu asanu aja adaŵatulutsadi, mfumu ya ku Yerusalemu, ya ku Hebroni, ya ku Yaramuti, ya ku Lakisi ndi ya ku Egiloni. Mafumu ameneŵa atabwera nawo kwa Yoswa, iye adaitana Aisraele onse. Ndipo adalamula akuluakulu ake amene adapita naye limodzi kuti, “Bwerani kuno, muŵaponde pa khosi mafumu ameneŵa, kusonyeza kuti agonjetsedwa.” Iwo adabweradi, naŵaponda pa khosi. Tsono Yoswa adauza akuluakuluwo kuti, “Musaope kapena kutaya mtima. Mukhale amphamvu ndiponso mulimbe mtima, poti Chauta adzaŵachita zimenezi adani anu onseŵa.” Pamenepo Yoswa adapha mafumu onsewo naŵapachika pa mitengo isanu, ndipo adakhala pa mitengo imeneyo mpaka madzulo. Dzuŵa litangoloŵa, Yoswa adalamula kuti atsitse mafumu aja pamitengopo, ndipo kuti aikidwe m'phanga lomwe ankabisalamolo. Tsono pa khomo la phangalo adatsekapo ndi miyala ikuluikulu, ndipo ikali pomwepo mpaka lero lino. Tsiku lomwelo Yoswa adathira nkhondo mzinda wa Makeda naugwira pamodzi ndi mfumu yake. Adapha onse amumzindamo, ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe wotsala wamoyo. Mfumu ya ku Makeda adaichita zomwe adaichita mfumu ya ku Yeriko. Tsono Yoswa pamodzi ndi Aisraele adapitirira kuchokera ku Makeda nakafika ku Libina, nauthira nkhondo mzindawo. Ndipo Chauta adapereka mzindawo m'manja mwa Aisraele. Adakantha munthu aliyense mumzindamo ndi lupanga, osasiyapo ndi mmodzi yemwe. Mfumu ya mzindawo adaichita zomwe adaichita mfumu ya ku Yeriko. Zitatha zimenezi, Yoswa pamodzi ndi ankhondo ake adapitirira kuchokera ku Libina mpaka ku Lakisi. Adazinga mzindawo ndi kuuthira nkhondo. Chauta adapatsa Aisraele mphamvu zogonjetsera mzinda wa Lakisi pa tsiku lachiŵiri la nkhondoyo. Tsono monga momwe adachitira ku Libina, sadapulumutsepo ndi mmodzi yemwe, koma adapha onse. Pamenepo Horamu, mfumu ya ku Gezere, anadza kudzathandiza Lakisi, koma Yoswa adamgonjetsa pamodzi ndi anthu ake omwe, osasiyapo wamoyo ndi mmodzi yemwe. Pambuyo pake Yoswa pamodzi ndi ankhondo ake adapitirira ku Lakisi mpaka ku Egiloni. Adazinga mzinda wa Egiloniwo ndi kuuthira nkhondo. Adaugonjetsa tsiku limodzi lomwelo, napha onse amumzindamo monga momwe adachitira ku mzinda wa Lakisi uja. Tsono Yoswa ndi ankhondo ake adapitirira ku Egiloni mpaka kubzola mapiri, ndi kukafika ku mzinda wa Hebroni. Adauthira nkhondo, mpaka kuugonjetsa. Adapha ndi lupanga mfumu pamodzi ndi anthu onse amumzindamo, ndi onse a m'midzi yapafupi omwe. Tsono Yoswa adalamula kuti mzindawo auwononge, monga momwe adachitira mzinda wa Egiloni. Palibe ndi mmodzi yemwe m'menemo amene adatsala wamoyo. Pamenepo Yoswa pamodzi ndi ankhondo ake adatembenukira mzinda wa Debiri, ndipo adauthira nkhondo. Adaugonjetsa naulanda pamodzi ndi mfumu yake, kudzanso midzi yoyandikana nawo. Adapha anthu onse akumeneko. Yoswa adauchita mzinda wa Debiri zomwe adauchita mzinda wa Hebroni ndi Libina pamodzi ndi mafumu ake. Choncho Yoswa adagonjetsa dziko lonselo. Adagonjetsa mafumu onse m'dziko lamapiri lija, m'dziko lakumwera, m'dziko lakuchigwa ndi lamagomo. Sadasiyepo ndi mmodzi yemwe, koma adapha onse. Zimenezi ndi zimene Chauta, Mulungu wa Aisraele, adalamula. Yoswa adagonjetsa adani onse kuyambira ku Kadesi-Baranea chakumwera, mpaka ku Gaza kufupi ndi nyanja, kuphatikizapo dziko lonse la Goseni mpaka ku Gibiyoni. Yoswa adagonjetsa mafumu onseŵa pamodzi ndi dziko lao lonse kamodzinkamodzi, chifukwa choti Chauta, Mulungu wa Aisraele, ndiye amene ankaŵamenyera nkhondoyo. Zitatha zimenezi, Yoswa pamodzi ndi ankhondo ake adabwerera ku zithando zao ku Giligala. Mbiri ya zimene zinkachitikazi idamfika Yabini, mfumu ya ku Hazori. Motero iyeyo adatumiza uthenga kwa Yobabu mfumu ya ku Madoni, ndiponso kwa mafumu a ku Simironi ndi Akisafu. Adatumizanso uthenga kwa mafumu a ku dziko lamapiri kumpoto kwa chigwa cha Yordani, kumwera kwa nyanja ya Galilea, m'dziko la chigwa cha Yordani ndiponso kumbali kwa nyanja, kufupi ndi Dori. Adatumizanso uthenga kwa Akanani a pa mbali zonse ziŵiri za Yordani, kwa Aamori, Ahiti, Aperizi ndi Ayebusi a ku dziko lamapiri, mpakanso kwa Ahivi amene ankakhala patsinde pa phiri la Heremoni m'dziko la Mizipa. Mafumuwo adabwera ndi ankhondo ao onse, ndipo kuchuluka kwao kwa ankhondowo kunali ngati mchenga wa m'mbali mwa nyanja. Anali ndi akavalo ambiri, pamodzi ndi magaleta omwe. Mafumu onseŵa adasonkhana pamodzi, nakamanga zithando ku mtsinje wa Meromu, kuti alimbane ndi Aisraele. Chauta adauza Yoswa kuti, “Usaŵaope amenewo. Maŵa pa nthaŵi yonga yomwe ino, adzaphedwa onsewo. Akavalo ao muŵalumaze, ndipo mutenthe magaleta ao.” Motero Yoswa pamodzi ndi anthu ake adaŵathira nkhondo modzidzimutsa ku mtsinje wa Meromu. Chauta adapatsa Aisraelewo mphamvu zogonjetsera adaniwo, mwakuti adaŵapambana kwenikweni, naŵapirikitsa mpaka kumpoto ku Sidoni Wamkulu ndi ku Misirefoti-Maimu ndiponso kuvuma, ku chigwa cha Mizipa. Adapha onsewo, osatsala ndi mmodzi yemwe. Yoswa adangoŵachita zomwe Chauta adalamula. Adalumaza akavalo, natentha magaleta. Pambuyo pake Yoswa adabwera nagonjetsa mzinda wa Hazori ndi kupha mfumu yake. Nthaŵi imeneyo nkuti mzinda wa Hazori uli wamphamvu kupambana maufumu ena onse. Adapha aliyense kumeneko osasiya wamoyo ndi mmodzi yemwe, ndipo mzinda wonsewo adauthira moto. Yoswa adagwira mafumu onsewo pamodzi ndi mizinda yao yomwe. Adalamula kuti aphedwe onsewo, potsata lamulo la Mose mtumiki wa Mulungu. Komabe Aisraelewo sadatenthe mizinda yomangidwa pa magomo, kupatula mzinda wa Hazori umene Yoswa adauthira moto. Tsono Aisraele adafunkha zinthu zonse zabwino za m'mizinda imeneyo, pamodzi ndi zoŵeta zomwe monga ng'ombe, nazisunga kuti zikhale zao. Koma adani okha adaphedwa onse, osatsala ndi mmodzi yemwe. Monga momwe Chauta adaalamulira mtumiki wake Mose, momwemo Moseyo adapereka malamulowo kwa Yoswa, ndipo Yoswa adachitadi zonse zimene Chauta adalamula Mose. Yoswa adagonjetsa dziko lonse, kuyambira dziko lamapiri, dziko lonse la Negebu lakumwera, dziko lonse la Goseni, chigwa chonse, dziko la Araba, dziko lonse la Israele lamapiri ndi chigwa chake chomwe, kuchokera ku phiri la Halaki kufupi ndi Seiri mpaka ku Baala-Gadi m'chigwa cha Lebanoni, kumwera kwa phiri la Heremoni. Adapha mafumu ao onse, atalimbana nawo nthaŵi yaitali. Palibe ndi mfumu imodzi yomwe imene idakambirana zamtendere ndi Aisraele, kupatula Ahivi okha amene ankakhala ku Gibiyoni. Koma ena onse adachita choŵagonjetsa ndi nkhondo. Chauta adaŵalimbitsa mtima iwowo kuti alimbane ndi Aisraele, kuti motero aonongeke onse, ndipo aphedwe mopanda chifundo. Zimenezi ndizo zimene Chauta adaalamula Mose. Nthaŵi imeneyi nkuti Yoswa atapita kukaonongeratu mtundu wa Aanaki. Iwowo anali kukhala m'dziko lija lamapiri, monga ku Hebroni, ku Debiri, ku Anabu ndi ku maiko onse amapiri aja a Yuda ndi a Israele. Yoswa adaŵaononga kwathunthu onsewo ndi mizinda yao yomwe. Palibe ndi Mwanakimu mmodzi yemwe amene adatsalako m'dziko lonse la Aisraele, komabe ku Gaza, ku Gati ndi ku Asidodi adatsala pang'ono. Choncho Yoswa adagonjetsa dziko lonselo potsata mau amene Chauta adaalamula Mose. Chauta adapereka dziko kwa Aisraele kuti likhale lao, ndipo adaligaŵagaŵa kuti fuko lililonse likhale ndi gawo lake. Motero anthu onse adapumula osamenyanso nkhondo. Aisraele anali atagonjetsa dziko lonse la kuvuma kwa Yordani, kuyambira ku chigwa cha Arinoni m'chigwa cha Yordani, mpaka kumpoto ku phiri la Heremoni ndi dera lonse la kuvuma kwa Araba, ndipo adakhazikika pa dziko lonselo. Mafumu amene adaŵagonjetsawo ndi aŵa, Sihoni mfumu ya Aamori amene ankakhala ku Hesiboni. Iyeyu ankalamulira kuyambira ku Aroere, mzinda umene uli pafupi ndi mtsinje wa Arinoni, mpaka ku mtsinje wa Yaboki ku malire a dziko la Aamoni, ndiponso kuphatikizapo theka la dera la Giliyadi. Dzikolo lidaphatikizaponso chigwa cha Yordani, kuyambira kumwera kwa nyanja ya Galilea, kumapita cha ku Beteyesimoti, mzinda umene uli pafupi pa Nyanja Yakufa, mpaka kumwera ndithu, patsinde pa phiri la Pisiga. Aisraele adagonjetsanso Ogi, mfumu ya ku Basani, amene anali mmodzi mwa otsala a Arefaimu. Iyeyu ankakhala ku Asitaroti ndi ku Ederei. Ufumu wake unkafika mpaka ku phiri la Heremoni ndi ku Saleka, ndi ku Basani yense, mpaka ku malire a Agesuri ndi a Amakati. Ufumuwo unkaphatikizanso theka la Giliyadi, kufikira ku dziko la Sihoni mfumu ya Hesiboni. Mose pamodzi ndi Aisraele adaaŵagonjetsa onsewo, ndipo Mose mtumiki wa Chauta adaapereka maiko aoŵa kwa fuko la Rubeni ndi la Gadi, ndiponso kwa theka la fuko la Manase, kuti akhale choloŵa chao. Yoswa ndi Aisraele anali atagonjetsa mafumu onse okhala m'dziko la kuzambwe kwa Yordani, kuyambira ku Bala-Gadi m'chigwa cha Lebanoni, mpaka ku phiri la Halaki, kumapita cha ku Seiri. Yoswa adagaŵira mafuko a Aisraele dziko limenelo, kuti likhale choloŵa chao. Dziko limenelo lidaali lamapiri, lachipululu, ndiponso dziko louma lakumwera. M'dziko limeneli ndimo m'mene munkakhala Ahiti, Aamori, Akanani, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi. Mafumu amene adagonjetsedwawo ndi aŵa: mafumu a ku Yeriko, Ai pafupi ndi Betele, Yerusalemu, Hebroni, Yaramuti, Lakisi, Egiloni, Gazere, Debiri, Gederi, Horoma, Aradi, Libina, Adulamu, Makeda, Betele, Tapuwa, Hefere, Afeki, Lasaroni, Madoni, Hazori, Simironi-Meroni, Akisafu, Tanaki, Megido, Kedesi, Yokoneamu (m'Karimele), Dori (m'mbali mwa nyanja), Goimu (m'Galilea), ndi Tiriza. Mafumu onse analipo 31. Nthaŵi imeneyo Yoswa anali atakalamba kwambiri. Tsono Chauta adamuuza kuti, “Tsopanotu iwe wakalamba kwambiri, koma dziko losalandidwa likalipo lalikulu. Maiko amene atsalako ndi aŵa: dziko lonse la Afilisti, ndi dziko lonse la Gesuri, (dziko limene layambira ku mtsinje wa Sihori kuvuma kwa Ejipito mpaka ku malire a Ekeroni, lonselo lili m'manja mwa Akanani. Olamulira dziko la Afilisti akukhala ku Gaza, ku Asidodi, ku Asikeloni, ku Gati ndi ku Ekeroni), ndiponso dziko la Avimu chakumwera. Palinso dziko la Akanani ndi la Meala, lomwe lili m'manja mwa Asidoni mpaka ku Afeki, malo amene ali pafupi ndi malire a Aamori. Palinso dziko lonse la Gebala ndi la Lebanoni chakuvuma, kuchokera ku Balagadi patsinde pa phiri la Heremoni mpaka ku Hamatipasi. Palinso dziko la Asidoni, amene akukhala m'dera lamapiri, pakati pa phiri la Lebanoni ndi la Misirefoti-Maimu. Anthu onsewo Ine Mulungu ndidzaŵapirikitsa m'mene Aisraele azikafika. Uŵagaŵire Aisraele maiko ameneŵa kuti akhale choloŵa chao, potsata zomwe ndakulamula. Tsono ugaŵe maiko ameneŵa pakati pa mafuko asanu ndi anai ndi theka lina lija la fuko la Manase, kuti akhale choloŵa chao.” Anthu a fuko la Rubeni ndi la Gadi ndiponso theka lina lija la fuko la Manase adalandira dziko lao cha kuvuma kwa Yordani. Dziko limeneli ndilo lija adaŵapatsa Mose mtumiki wa Chauta. Dziko laolo lidayambira ku Aroere, mzinda umene uli pafupi ndi chigwa cha Arinoni, ndiponso ku mzinda wokhala pakati pa chigwacho. Dzikolo linkaphatikiza dera lonse lokwera kuyambira ku Medeba kukafika ku Diboni. Linkaphatikizaponso mizinda yonse yomwe inkalamulidwa ndi Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankalamula ku Hesiboni, mpaka ku malire a Aamoni. Lidaphatikizaponso Giliyadi ndi dziko limene Agesuri ndi Amakati ankakhalamo, kudzanso phiri lonse la Heremoni, pamodzi ndi Basani, mpaka ku Saleka. Ndipo ku Basani lidaphatikizapo dziko la Ogi amene ankalamula ku Asitaroti ndi ku Ederei. (Ogi anali yekhayo mfumu ya Arefaimu amene adatsalako). Mose anali atagonjetseratu anthu ameneŵa ndi kuŵapirikitsira kutali. Koma Aisraele sadapirikitse Agesuri ndi Amakati. Anthu ameneŵa akadalipo pakati pa Aisraele. Komabe Mose sadapereke dziko kwa fuko la Levi. Zimene ankalandira iwowo ngati choloŵa chao ndi gawo la zopereka zopsereza zimene anthu ankapereka kwa Chauta, monga momwe Chauta adaauzira Mose. Mose adapereka gawo lina la dziko kwa mabanja a fuko la Rubeni kuti likhale choloŵa chao. Dziko laolo lidayambira ku Aroere, mzinda umene uli pafupi ndi chigwa cha Arinoni, ndiponso mzinda wokhala pakati pa chigwacho, ndiponso dera lonse lokwera kuyambira ku Medeba, kuphatikizapo Hesiboni, pamodzi ndi mizinda yonse ya ku chigwa monga: Diboni, Bamoti-Baala, Bete-Baala-Meyani, Yahazi, Kedemoti, Mefaati, Keriyataimu, Sibima, Zeretisahara pa phiri la m'chigwa, Betepeori, matsitso onse a phiri la Pisiga ndi Beteyesimoti. Imeneyi ndiyo mizinda yonse yakuchigwa, mizinda yonse ya Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankalamulira ku Hesiboni. Mose anali atagonjetsa Sihoni pamodzi ndi onse olamulira ku Midiyani monga: Evi, Rekemu, Zeri, Huri ndi Reba. Onseŵa ankalamulira dzikolo ngati anyakwaŵa a Sihoni. Pakati pa ophedwa ndi Aisraele panali Balamu, mwana wa Beori, wolosa zakutsogolo uja. Mtsinje wa Yordani ndiwo unali malire a fuko la Rubeni. Mizinda imeneyo pamodzi ndi midzi yake ndi imene idapatsidwa kwa mabanja a fuko la Rubeni, kuti ikhale choloŵa chao. Gawo lina la dzikolo, Mose adalipatsa mabanja a fuko la Gadi, kuti likhale choloŵa chao. Dziko laolo lidaphatikiza Yazere pamodzi ndi mizinda ya Giliyadi, hafu lonse la dziko la Aamoni mpaka ku Aroere, kuvuma kwa Raba. Lidayambira ku Hesiboni mpaka ku Ramati-Mizipe ndi Betonimu, kuchokeranso ku Mahanaimu mpaka ku malire a Lodebara. M'chigwa cha Yordani adalandiramo Beteharamu, Betenimura, Sukoti ndi Safoni, kudzanso theka la dziko la Sihoni, mfumu ya ku Hesiboni. Malire ake akuzambwe anali mtsinje wa Yordani kufikira ku nyanja ya Galilea chakumpoto. Mizinda imeneyi, pamodzi ndi midzi yake, ndiyo imene idapatsidwa kwa mabanja a fuko la Gadi, kuti ikhale choloŵa chao. Mose anali atapereka kale gawo lina la dziko kwa mabanja a theka la fuko la Manase lija, kuti likhale choloŵa chao. Dzikolo lidayambira ku Mahanaimu kuphatikizapo dziko lonse la mfumu Ogi, mfumu ya ku Basani, pamodzi ndi midzi 60 ya ku Yairo, ku Basaniko. Lidaphatikizaponso theka la Giliyadi, pamodzi ndi Asitaroti ndi Ederei, mizinda yaikulu ya mfumu Ogi wa ku Basani. Mizinda imeneyi idapatsidwa kwa mabanja a Makiri mwana wa Manase, kuti ikhale choloŵa cha hafu la Amakiri malinga ndi mabanja ao. Umu ndimo m'mene Mose adagaŵira dziko la m'zigwa za Mowabu, kuvuma kwa Yeriko, kutsidya kwa Yordani. Komatu Mose sadaŵapatse dziko a fuko la Levi. Mose adaŵauza Aleviwo kuti choloŵa chao ndi gawo la zopereka zimene anthu ankapereka ngati nsembe zopsereza kwa Chauta, monga momwe Chautayo adaauzira Mose. Maiko amene Aisraele adalandira ku Kanani adagaŵidwa motere: Wansembe Eleazara, Yoswa mwana wa Nuni, ndi atsogoleri a mabanja a mafuko a Aisraele, onseŵa ndiwo adagaŵa maikowo, kugaŵira Aisraele. Potsata zimene Mulungu adalamula Mose, dziko lonse lidagaŵidwa mwamaere kwa mafuko asanu ndi anai ndi theka. Mose adagaŵira mafuko aŵiri ndi theka aja magawo ao a dziko kuvuma kwa Yordani, koma Alevi okha sadaŵagaŵire. Tsono fuko la Yosefe adaligaŵa paŵiri, Manase ndi Efuremu. Alevi sadalandire gawo lililonse la dziko. Adangolandira mizinda kuti azikhalamo ndi timaiko todyetsamo zoŵeta zao. Aisraelewo adangogaŵana dzikolo potsata zimene Chauta adaalamula Mose. Anthu a fuko la Yuda adabwera kwa Yoswa ku Giligala. Kalebe mmodzi mwa iwowo, mwana wa Yefune Mkenizi, adauza Yoswa kuti, “Inu mukudziŵa zimene Chauta adauza Mose, munthu wa Mulungu uja, za inu ndi ine ku Kadesi-Baranea. Nthaŵi imene ija ndinali ndi zaka makumi anai pamene Mose mtumiki wa Chauta adandituma kuchokera ku Kadesi-Baranea kukazonda dziko lija. Nditabwerako, ndidamuuzadi zoona zonse zimene ndidaona. Komabe anthu amene anali nane pa ulendowo, adachititsa mantha anthu. Koma ine ndidamvera mokhulupirika Chauta, Mulungu wanga. Pamenepo Mose adandilonjeza kuti, ‘Chifukwa choti wamvera mokhulupirika Chauta, Mulungu wanga, iweyo pamodzi ndi ana ako, udzalandiradi dziko limene walipondalo, kuti likhale choloŵa chako.’ ” Kalebe adapitiriranso kunena kuti, “Koma tsopano, papita zaka 45 Chauta atauza kale Mose zimenezi. Taonani, ndili ndi zaka 85 tsopano, komabe ndikadali ndi mphamvu lero, monga ndidaaliri muja, pamene Mose adandituma. Ndikadali wamphamvu, mwakuti ndingathe kumenya nkhondo ndithu, ndiponso ndingathe kuchita zina zonse. Tsopano mundigaŵire dziko lamapiri lomwe Chauta adandilonjezeratu. Paja mudamva kuti Aanaki, anthu amphamvu, adalipodi kumeneko m'mizinda yao yamalinga. Komabe mwina Chauta adzakhala nane, ndipo ndidzaŵapirikitsa monga momwe Chauta adanenera.” Pamenepo Yoswa adadalitsa Kalebe, mwana wa Yefune, nampatsa Hebroni kuti likhale dziko lake. Mpaka lero lino dziko la Hebroni ndi la zidzukulu za Kalebe, mwana wa Yefune Mkenizi, poti adamvera mokhulupirika Chauta, Mulungu wa Aisraele. Zisanachitike zimenezi, Hebroni ankatchedwa Kiriyati-Ariba. Arabayo ndiye anali wotchuka kopambana pakati pa Aanaki. Pambuyo pake m'dziko lonselo mudakhala mtendere. Mabanja onse a fuko la Yuda adalandira chigawo cha dzikolo motero: dziko lao lidalekeza ku malire a Edomu, mpaka ku chipululu cha Zini, kumwera kwenikweni. Malire ake akumwera adayambira kumwera kwenikweni kwa Nyanja Yakufa, napita cha kumwera kokhakokha kuyambira ku chikweza cha ku Akarabimu, nkudzera pa mpata wa mapiri a ku Zini. Kuchokera kumeneko, adabzola cha kumwera kwa Kadesi-Baranea, kupitirira Hezironi mpaka ku Adara, ndi kutembenukira ku Karaka. Adapitirira mpaka ku Azimoni, natsata mtsinje wa m'malire a Ejipito mpaka ku nyanja. Ameneŵa ndiwo malire akumwera. Malire akuvuma anali Nyanja Yakufa mpaka kumene Yordani amathira m'Nyanja Yakufa. Tsono malire akumpoto adayambira kunyanjako, napitirira mpaka ku Betehogila, nakafika kumpoto kwa Betaraba. Adapitirira mpaka kukafika ku Mwala wa Bohani, mwana wa Rubeni. Ndipo malirewo adachokeranso ku chigwa cha Mavuto mpaka ku Debiri, mpakanso kumpoto kuloŵera ku Giligala, kuyang'anana ndi chikweza cha Adumimupasi cha ku mbali yakumwera ya chigwa. Tsono adapitiriranso ku akasupe a Enisemesi, natulukira ku Enirogele. Ndipo adakwera kubzola chigwa cha mwana wa Hinomu cha mbali ya kumwera kwa Ayebusi, (ndiye kuti ku Yerusalemu). Malirewo adapitirira kukafika pamwamba pa phiri moyang'anana ndi chigwa cha Hinomu chakuzambwe, ku mathero akumpoto a chigwa cha Refaimu. Tsono adachokeranso pamwamba pa phiri, nakafika mpaka ku akasupe a Nepitowa, nadzatulukira ku mizinda ya ku phiri la Efuroni. Kuchoka uko nkutsikira ku Baala, (ndiye kuti Kariyati-Yearimu), kumene adazungulira cha kuzambwe kwa Baala, kuloza ku dziko lamapiri la Seiri. Adapitirira cha kumpoto kutsata phiri la Yearimu, (ndiye kuti Kesaloni), natsikira ku Betesemesi mpaka kubzola Timna. Tsono malirewo adatulukira ku matsitso a phiri cha kumpoto kwa Ekeroni. Adakhotera ku Sikeroni, kubzola phiri la Baala, mpaka kukafika ku Yabinele. Malire amenewo adakathera ku nyanja. Kuzambwe malire anali gombe la Nyanja Yaikulu yomwe. Ameneŵa ndiwo malire amene adazungulira maiko opatsidwa kwa fuko la Yuda. Monga momwe Chauta adalamulira Yoswa, gawo lina la dziko la fuko la Yuda lidapatsidwa kwa Kalebe mwana wa Yefune. Yoswa adampatsa Kiriyati-Ariba ndiye kuti Hebroni. (Araba anali bambo wa Anaki). Kalebe adapirikitsa mafuko atatu a Anaki m'dzikomo, maina ao ndi aŵa: Sesai, Ahimani ndi Talimai. Kuchokera kumeneko adapita kukalimbana ndi anthu a ku Debiri. Mzinda umenewu kale unkatchedwa Kiriyati-Sefere. Tsono Kalebe adati, “Mkulu wa ankhondo amene athire nkhondo mzinda wa Kiriyati-Sefere, naulanda, ndidzampatsa mwana wanga Akisa kuti akhale mkazi wake.” Mbale wake wa Kalebe, Otiniyele, mwana wa Kenazi, adaulanda mzindawo. Choncho Kalebe adampatsa mwana wake Akisa kuti akhale mkazi wake. Tsiku lina, Akisayo atafika, Otiniyele adaumiriza mkazi wakeyo kuti apemphe munda kwa Kalebe bambo wake. Tsono Akisa atatsika pa bulu wake, Kalebe adamufunsa kuti, “Kodi ukufuna kanthu?” Iye adayankha kuti, “Ndimati mundipatseko mphatso. Popeza kuti mwandikhazika m'dziko la Negebu lopanda madzi, mundipatsenso akasupe a madzi.” Choncho Kalebe adampatsa akasupe akumtunda ndi akuchigwa omwe. Ili ndilo dziko limene mabanja a fuko la Yuda adalandira ngati choloŵa chao. Mizinda ya kumwera kwenikweni imene iwo adalandira yoyandikana ndi dziko la Edomu, inali iyi: Kabizeele, Edere, Yaguru, Kina, Dimona, Adada, Kedesi, Hazori, Itinani, Zifi, Telemu, Bealoti, Hazori-Hadata, Keriyoti-Hezironi, (ndiye kuti Hazori), Amama, Sema, Molada, Hazaragada, Hesimoni, Betepeleti, Hazara-Suwala, Beereseba, Biziyotiya, Baala, Iyimu, Ezemu, Elitoladi, Kesili, Horoma, Zikilagi, Madimana, Sanisana, Lebaoti, Silihimu, Aini ndi Rimoni. Yonse inalipo mizinda 29, pamodzi ndi midzi yake yozungulira yomwe. Mizinda yakuchigwa inali iyi: Esitaoli, Zora, Asina, Zanowa, Enganimu, Tapuwa, Enamu, Taramuti, Adulamu, Soko, Azeka, Saraimu, Aditaimu, Gedera ndi Gederotaimu. Yonse inalipo mizinda 14, pamodzi ndi midzi yake yozungulira. Panalinso Zenani, Hadasa, Megidali-Gadi, Dileani, Mizipa, Yokotele, Lakisi, Bozikati, Egiloni, Kaboni, Lahamasi, Kitilisi, Gederoti, Betedagoni, Naama ndiponso Makeda. Yonse inali mizinda 16, pamodzi ndi midzi yake yozungulira. Panalinso Libina, Eteri, Asani, Ifuta, Asana, Nezibu, Keila, Akizibu ndi Maresa. Yonse inali mizinda isanu ndi inai, pamodzi ndi midzi yake yozungulira. Panalinso Ekeroni ndi midzi yake. Yonse imene inali m'mbali mwa Nyanja Yaikulu, kuchokera ku Ekeroni mpaka ku Asidodi. Adalandiranso mizinda yaikulu ya Asidodi ndi Gaza, pamodzi ndi midzi yake yozungulira. Malire ake adafika ku mtsinje wa ku Ejipito, ndipo mpaka ku Nyanja Yaikulu. Ku dziko lakumapiri kunali Samiri, Yatiri, Soko, Dana, Kiriyati-Sana, (ndiye kuti Debiri), Anabu, Esitemowa, Animu, Goseni, Holoni ndi Gilo. Yonse inalipo 11, pamodzi ndi midzi yake yozungulira. Panalinso Arabu, Duma, Esani, Yanimu, Betetapuwa, Afeka, Humata, Kiriyati-Ariba (ndiye kuti Hebroni), ndi Aziyori. Yonse inalipo isanu ndi inai, pamodzi ndi midzi yake yozungulira. Panalinso Maoni, Karimele, Zifi, Yuta, Yezireele, Yokodeamu, Zanowa, Kaini, Gibea ndi Timna. Yonse inalipo mizinda khumi, pamodzi ndi midzi yake yozungulira. Panalinso Halahulu, Betezuri, Gedori, Maarati, Betanoti ndi Elitekoni. Yonse inalipo mizinda isanu ndi umodzi, kuphatikizapo midzi yake yozungulira. Panalinso Kiriyati-Baala (ndiye kuti Kiriyati-Yearimu) ndi Raba. Yonse inalipo mizinda iŵiri, pamodzi ndi midzi yake yozungulira. Mizinda yam'chipululu inali Betaraba, Midini, Sekaka, Nibisani, mzinda wa Mchere ndi Engedi. Yonse inalipo mizinda isanu ndi umodzi, pamodzi ndi midzi yake yozungulira. Koma anthu a fuko la Yuda sadathe kupirikitsa Ayebusi amene ankakhala ku Yerusalemu. Ndipo mpaka pano Ayebusiwo amakhalabe mu Yerusalemu, pamodzi ndi anthu a fuko la Yuda. Dziko limene lidapatsidwa kwa zidzukulu za Yosefe lidayambira ku mtsinje wa Yordani pafupi ndi Yeriko, cha kuvuma kwa akasupe a Yeriko, kukaloŵa m'chipululu. Lidayambiranso ku Yeriko, ndi kukaloŵa m'dziko lamapiri chakuzambwe, mpaka kukafika ku chipululu cha Betele. Kuchokera ku Betele malire ake adakafika ku Luzi, nabzola ku Ataroti kumene kunkakhala Aaraki. Tsono lidapitirira ndithu kuzambwe, kudera la Ayafaleti, mpaka kufika kunsi kwa Betehoroni. Kuchokera kumeneko malire ake adalunjika ku Gezere, nakalekeza mpaka ku nyanja. Choncho ana a Yosefe, Manase ndi Efuremu adalandira choloŵa chao. Dziko la mabanja a Efuremu ndi ili: malire ake akuvuma anali Ataroti-Adara mpaka kukafika kumtunda kwake kwa Betehoroni. Kuchokera kumeneko malirewo adatsikira mpaka ku nyanja. Mikimetati anali kumpoto kwake. Kuvuma malirewo adakhotera cha ku Taanatisilo, napitirira malo amenewo chakuvuma, mpaka kukafika ku Yanowa. Tsono kuchokera ku Yanowa, adatsikira ku Ataroti ndi ku Naara. Adakafika ku Yeriko ndi kukathera m'Yordani. Malirewo adaloŵera kuzambwe kuchokera ku Tapuwa mpaka ku mtsinje wa Kana, ndi kutsikira mpaka ku nyanja. Dziko limenelo ndilo lidapatsidwa kwa mabanja a Aefuremu kuti likhale choloŵa chao, kuphatikizapo mizinda ndi midzi yopatsidwa kwa Aefuremu, koma yokhala m'kati mwa dziko la anthu a fuko la Manase. Komatu Akanani amene ankakhala ku Gezere, Aefuremu sadaŵapirikitse, kotero kuti Akanani ameneŵa alipobe pakati pa Aefuremu mpaka lero lino. Komabe Akananiwo ankakakamizidwa kugwira ntchito yathangata. Gawo lina la dzikolo lidapatsidwa kwa fuko la Manase amene anali mwana wachisamba wa Yosefe. Makiri, kholo la anthu okhala ku Giliyadi, ndiye anali mwana wachisamba wa Manase. Makiri analinso msilikali, motero maiko aŵa, Giliyadi ndi Basani, adapatsidwa kwa iyeyo. Mabanja otsala a Manase amene adapatsidwanso dziko ndi aŵa: Abiyezere, Heleki, Asiriele, Sekemu, Hefere ndi Semida. Ameneŵa ndiwo zidzululu za Manase, mwana wa Yosefe, komanso ndiwo amene anali eni mbumba. Panali Zelofehadi mwana wa Hefere, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase. Zelofehadiyo analibe mwana wamwamuna ndi mmodzi yemwe, koma aakazi okhaokha. Maina a ana aakaziwo ndi aŵa: Mahala, Nowa, Hogola, Milika ndi Tiriza. Iwoŵa adabwera kwa Eleazara wansembe, nafikanso kwa Yoswa mwana wa Nuni ndi kwa atsogoleri, ndipo adati, “Chauta adalamula Mose kuti ife ndi alongo athu atipatse gawo lina la dziko ngati choloŵa chathu.” Motero iwowo, pamodzi ndi abale a bambo wao, adapatsidwa dziko kuti likhale lao potsata zimene Chauta adalamula. Choncho kuwonjeza pa maiko a Giliyadi ndi Basani a kuvuma kwa Yordani, a fuko la Manase adalandiranso magawo khumi, popeza kuti ana aakazi a Manase ndi ana ake aamuna, onsewo adalandira magawo ao. Dziko la Giliyadi lidapatsidwa kwa otsala mwa zidzukulu za Manase. Dziko la Manase malire ake adachokera ku Asere, ndipo adakafika ku Mikimetati kuvuma kwa Sekemu. Tsono malire adapita kumwera kuloza kwa anthu a ku Entapuwa. Dzikolo linali la Manase, koma mzinda wa Tapuwa wapamalire unali wa fuko la Efuremu, ngakhale kuti m'pakati penipeni pa mizinda ya Manase. Tsono malire ake adatsikira ku kamtsinje ka Kana. Mizinda yakumwera kwa kamtsinje kameneka inali ya fuko la Efuremu, ngakhale inali m'dziko la Manase. Malire a dziko la Manase adalambalala chakumpoto kwa kamtsinjeko, nakalekezera ku nyanja. Efuremu anali kumwera, Manase anali kumpoto, ndipo Nyanja Yaikulu inali malire akuzambwe. Malirewo adakafika ku Asere kumpoto chakuzambwe ndi ku Isakara kumpoto chakuvuma. M'dziko la Isakara ndi la Asere munalinso gawo lina la Manase lotchedwa Beteseani, kuphatikizapo midzi yozungulira. Panalinso Akanani amene ankakhala ku Ibleamu, ku Dori mzinda wa m'mbali mwa nyanja, ku Endori, ku Taana ndi ku Megido, pamodzi ndi midzi yake yozungulira. Komabe anthu a fuko la Manase sadathe kuŵapirikitsa Akanani okhala m'mizinda imeneyo. Motero Akananiwo adangokhalabe komweko. Ngakhale pamene Aisraele anali amphamvu m'dzikomo, sadapirikitse Akanani onse, koma adangoŵasandutsa anthu ogwira ntchito yathangata. Zidzukulu za Yosefe zidafunsa Yoswa kuti, “Bwanji ife mwangotigaŵira gawo limodzi lokha la dziko, kuti likhale choloŵa chathu? Ifetu tilipo ambiri chifukwa Chauta adatidalitsa.” Yoswa adaŵayankha kuti, “Ngati mulipo ambiri, ndipo ngati dziko lamapiri la Efuremulo likucheperani, loŵani ku nkhalango, mudule mitengo ndi kudzikonzera malo oti mukhalepo m'dziko la Aperizi ndi Arefaimu.” Pamenepo zidzukulu za Yosefezo zidati, “Zoonadi dziko lamapirilo silingatikwanire ife, komanso Akanani amene ali ku zigwa ali ndi magaleta achitsulo, ngakhale amene ali ku Beteseani ndi ponse pozungulira, ndiponso amene ali m'chigwa cha Yezireele.” Yoswa adauza zidzukulu za Yosefe za m'fuko la Efuremu ndi la Manase kuti, “Inu mulipo ambiri zedi ndipo ndinu amphamvu. Mudzalandira magawo enanso. Mudzalandiradi dziko lamapirilo. Ngakhale lili ndi nkhalango, inuyo mudzadula mitengo, ndipo mudzalandira dziko lonselo kuti likhale lanu. Akanani mudzaŵapirikitsa, ngakhale ali ndi magaleta achitsulo ndiponso ngakhale iwo ngamphamvu.” Ataligonjetsa dziko lonselo, Aisraele onse adasonkhana ku Silo, ndipo adamangako chihema chamsonkhano. Nthaŵi imeneyo nkuti mafuko asanu ndi aŵiri asanapatsidwe magawo ao a dzikolo. Motero Yoswa adafunsa Aisraele kuti, “Kodi mudzadikira mpaka liti kuti muloŵe m'dziko limene Chauta, Mulungu wa makolo anu, adakupatsani? Tandipatsani amuna atatu a fuko lililonse. Ameneŵa ndiŵatuma kuti akayendere dziko lonselo, ndipo alembe bwino magawo ake onse, kuti tithandizidwe poligaŵa. Atatero, abwererenso kuno kwa ine. Adzaligaŵe dzikolo magawo asanu ndi aŵiri. Yuda adzakhala m'dziko lake kumwera, ndipo Yosefe adzakhala m'dziko lake kumpoto. Mudzalembe mau ofotokoza za magawo asanu ndi aŵiriwo a dziko limenelo, ndi kudzandipatsa ine. Ineyo ndiye ndidzakuchitireni maere pamaso pa Chauta, Mulungu wathu. Alevi okha sadzalandira nao gawo la dzikolo, popeza kuti gawo lao ndi kutumikira Chauta pa unsembe. Fuko la Gadi ndi la Rubeni ndi theka la fuko la Manase adalandira kale dziko lao kuvuma kwa Yordani. Mose, mtumiki wa Chauta, ndiye adaŵapatsa.” Tsono anthuwo adapitadi kukalemba za dzikolo, Yoswa ataŵalangiza kuti, “Pitani, kaliyendereni dziko lonselo, ndipo mukalembe bwino za dzikolo. Tsono mutatero, mubwererenso kwa ine kuno. Ine ndidzakuchitirani maere pamaso pa Chauta konkuno ku Silo.” Pamenepo anthuwo adakaliyendera dziko lonselo, nalemba bwino m'buku za dzikolo. Adagaŵa dzikolo magawo asanu ndi aŵiri, ndipo adalembanso mndandanda wa midzi yonse. Atatero adabwerera kwa Yoswa ku zithando ku Silo kuja. Tsono Yoswa adachita maere, naŵapemphera nzeru kwa Chauta. Ndipo fuko lililonse la Aisraele adalipatsa gawo la dzikolo. Mabanja a fuko la Benjamini adalandira dziko la pakati pa Yuda ndi Yosefe. Kumpoto malire ao adayambira ku mtsinje wa Yordani, nakwera chitunda cha kumpoto kwa Yeriko nabzola dziko lamapiri chakuzambwe, nakafika ku chipululu cha Betaveni. Tsono malirewo adaloza ku Luzi, ndi kutsata mbali ya phiri loti Luzi, (lotchedwanso Betele). Tsono adatsikira ku Ataroti-Adara, kubzola phiri lili kumwera kwa Betehoroni wakunsi. Ndipo malirewo adaloŵanso kwina, nalunjika kumwera kuchokera kuzambwe kwake kwa phiri limene limayang'anana ndi Betehoroni, mpaka ku mzinda wa Kiriyati-Baala (wotchedwanso Kiriyati-Yeyarimu), mzinda wa fuko la Yuda. Ameneŵa ndiwo anali malire akuzambwe. Malire akumwera adayambira pamphepete penipeni pa Kiriyati-Yearimu, napita kuzambwe mpaka kukafika ku Akasupe a ku Nefutowa. Adatsikira m'mphepete mwa phiri limene limayang'anana ndi chigwa cha Benihinomu, cha kumpoto kwake kwa chigwa cha Arefaimu. Adapita chakumwera kubzola chigwa cha Hinomu, kumwera kwa chitunda cha Ayebusi, moyang'ana ku Enirogele. Tsono malire adakhota, naloŵa kumpoto ku Enisemesi ndi kubzola mpaka kukafika ku Geliloti, kuyang'anana ndi pokwerera pa Aduminu. Atatero malirewo adatsikira ku Mwala wa Bohani, mwana wa Rubeni. Adabzola cha kumpoto kwa chitunda cha Betaraba, natsikira ku chigwa cha Yordani. Adapitiriranso kumpoto kwa chitunda cha Betehogila, ndipo adakathera chakumpoto ku mathiriro a mtsinje wa Yordani m'Nyanja Yakufa, kumwera kwake kwenikweni kwa Yordani. Mtsinje wa Yordani ndiye udachita malire kuvuma kwake. Ameneŵa ndiwo anali malire a dziko limene mabanja a fuko la Benjamini adalandira, kuti likhale choloŵa chao. Mizinda ya mabanja a Benjamini inali Yeriko, Betehogila, Emekezizi, Betaraba, Zemaraimu, Betele, Avimu, Para, Ofura, Kefaramoni, Ofini ndi Geba. Yonse inalipo 12, pamodzi ndi midzi yake. Panalinso Gibiyoni, Rama, Beeroti, Mizipa, Kefira, Moza, Rekemu, Iripele, Tarala, Zela, Haelefe, Yebusi (ndiye kuti Yerusalemu), Gibea ndi Kiriyati-Yearimu. Yonse inalipo 14, pamodzi ndi midzi yake. Dziko limeneli ndilo limene mabanja a Benjamini adalandira, kuti likhale choloŵa chao. Mabanja a Simeoni adalandiranso gawo lao, Yoswa atachita maere kachiŵiri. Dziko lake linali m'kati mwenimweni mwa dziko la mabanja a Yuda. Ndipo lidaphatikiza Beereseba, Molada, Hazara-Suwala, Bala, Ezemu, Elitoladi, Betuli, Horoma, Zikilagi, Betemari-Kaboti, Hazarasusa, Betelebaoti ndiponso Saruheni. Yonse inalipo mizinda 13, pamodzi ndi midzi yake. Panalinso Aini, Rimoni, Eteri ndi Asani. Yonse inalipo mizinda inai, pamodzi ndi midzi yake. Imeneyi idaphatikizapo midzi yozungulira mizindayo, mpaka kukafika ku Baala-Tibere, ndiye kuti Rama wakumwera. Dziko limeneli ndi limene mabanja a fuko la Simeoni adalandira kukhala choloŵa chao. Gawo la Simeoni lidatapidwa ku gawo la Yuda, popeza kuti gawo la Yuda lidaali lalikulu kwambiri. Choncho choloŵa cha Simeoni chidatapidwa pa choloŵa cha Yuda. Mabanja a fuko la Zebuloni adalandira dziko lao, Yoswa atachita maere kachitatu. Dziko limene adalandiralo lidakafika mpaka ku Saridi. Tsono malirewo adakwera naloŵa kuzambwe ku Mareyala, nakafika ku Debeseti ndi ku mtsinje wa kuvuma kwa Yokoneamu. Pa mbali ina ya Saridi adapita chakuvuma ku malire a Kisiloti-Tabori, mpaka ku Debarati, nakafika ku Yafiya. Kuchokera kumeneko, adabzola naloŵa chakuvuma kumapita ku Gatihefere ndi ku Etikazini, kuloŵa ku Neya njira yaku Rimoni. Kumpoto malire amenewo adapita molunjika ku Hanatoni, nakathera ku chigwa cha Ifutahele. Adaphatikizapo Katati, Nahalala, Simironi, Idala ndi Betelehemu. Yonse inalipo mizinda 12, pamodzi ndi midzi yake. Mizinda imeneyi pamodzi ndi midzi yake inali m'dziko limene mabanja a fuko la Zebuloni adalandira ngati choloŵa chao. Mabanja a fuko la Isakara adalandira dziko lao, Yoswa atachita maere kachinai. Gawo lao lidaphatikiza Yezireele, Kesuloti, Sunemu, Hafaraimu, Siyoni, Anaharati, Rabiti, Kisiyoni, Ebezi, Remeti, Enganimu, Enihada ndi Betepazezi. Malire amenewo adakafikanso ku Tabori, Sahazuma ndi ku Betesemesi, ndi kutsikira ku Yordani. Lidaphatikiza mizinda 16 pamodzi ndi midzi yake. Mizinda imeneyi, pamodzi ndi midzi yakeyo, inali m'dziko limene mabanja a fuko la Isakara adalandira ngati choloŵa chao. Mabanja a fuko la Asere adalandira dziko lao, Yoswa atachita maere kachisanu. Gawo lake lidaphatikiza Helekati, Hali, Beteni, Akisafu, Alamumeleki, Amada ndi Misala. Kuzambwe malire adakafika ku Karimele ndi ku Sihori-Libinati. Adakhotera kuvuma naloŵera ku Betedagoni, nkukafika ku dziko la Zebuloni ndi ku chigwa cha Ifitaele pa njira yakumpoto, kumapita ku Betemeke ndi ku Neiyeli. Adabzola kupita kumpoto mpaka kukafika ku Kabulu, Ebroni, Rehobu, Hamoni ndi Kana, mpaka ku Sidoni wamkulu. Tsono malirewo adakhotera ku Rama, nakafika mpaka ku Tiro, mzinda wozingidwa ndi linga. Pamenepo adakhoteranso ku Hosa, nkukatulukira ku nyanja, m'dera la Akizibu, Uma, Afeki ndi Rehobu. Yonse pamodzi inalipo mizinda 22, pamodzi ndi midzi yake. Mizinda imeneyi, pamodzi ndi midzi yakeyo, inali m'dziko limene mabanja a fuko la Asere adalandira ngati choloŵa chao. Mabanja a fuko la Nafutali adalandira dziko lao, Yoswa atachita maere kachisanu ndi chimodzi. Malire ake adayambira ku Helefe kuchokera ku mtengo wogudira wa ku Zaananimu. Adachokeranso ku Adami-Nekebu ndi ku Yabinele mpaka ku Lakumu, nakathera ku Yordani. Ndipo malirewo adakhotera kuzambwe ku Azinoti-Tabori. Kuchoka kumeneko adaloŵera ku Hukoko, nakafika ku dziko la Zebuloni chakumwera, ndi ku dziko la Asere chakuzambwe, ndi ku mtsinje wa Yordani chakuvuma. Mizinda yamalinga inali iyi: Zidumu, Zeri, Hamati, Rakati, Kinereti, Adama, Rama, Hazori, Kedesi, Ederei, Enihazori, Yironi, Migidalele, Horemu, Betanati, ndi Betesemesi. Yonse inalipo mizinda 19, pamodzi ndi midzi yake. Mizinda imeneyi pamodzi ndi midzi yakeyo, inali m'dziko limene mabanja a fuko la Nafutali adalandira ngati choloŵa chao. Mabanja a fuko la Dani adalandira dziko lao, Yoswa atachita maere kachisanu ndi chiŵiri. Dziko laolo lidaphatikiza Zola, Esitaoli, Irisemesi, Saalabimu, Ayaloni, Itila, Eloni, Timna, Ekeroni, Eliteke, Gibetoni, Baalati, Yehudi, Beneberaki, Gatirimoni, Meyarikoni ndi Rakoni, ndiponso dziko loyang'anana ndi Yopa. Pamene anthu a fuko la Dani adalandidwa dziko lao, adapita nakathira nkhondo Lesemu, nagonjetseratu ndi kuwononga adani onse. Tsono atatero, adalanda mzindawo, nakhazikika kumeneko. Ndipo adasintha dzina la mzindawo kuti likhale Dani, pakuti limeneli linali dzina la kholo lao Dani. Mizinda imeneyi, pamodzi ndi midzi yake, inali m'dziko limene mabanja a fuko la Dani adalandira ngati choloŵa chao. Tsono Aisraele atatha kugaŵana zigawo zosiyanasiyana za dzikolo, adamgaŵirako Yoswa mwana wa Nuni dera lina la dzikolo kuti likhale choloŵa chake. Potsata zimene Chauta adalamula, adampatsako mzinda wa Timnati-Sera umene Yoswayo mwiniwake adaapempha, umene unali m'dziko la Efuremu lamapiri lija. Kumeneko ndiko kumene adamanga mzinda wake, nakhazikika komweko. Wansembe Eleazara, Yoswa mwana wa Nuni, pamodzi ndi atsogoleri amabanja a Aisraele, ndiwo amene adagaŵa dziko limeneli zigawozigawo, pochita maere pamaso pa Chauta. Ndipo ankachita zimenezi ku Silo, ku chipata choloŵera ku chihema chamsonkhano chija. Choncho adamaliza kuligaŵa dzikolo. Chauta adauza Yoswa kuti, “Uza Aisraele kuti, ‘Sankhulani mizinda yopulumukiramo, imene Ine ndidakuuzani kudzera mwa Mose. Munthu aliyense wopha mnzake mwangozi, osati mwadala, angathe kuthaŵira kumeneko. Motero angathe kupulumuka kwa wofuna kumlipsira. Angathe kuthaŵira ku umodzi mwa mizinda imeneyo, nakafika pa malo achiweruzo amene ali pa chipata cha mzindawo. Atafika, asimbire atsogoleri mlandu wakewo. Apo atsogoleriwo adzamlola kuloŵa mumzindamo, nadzampatsa malo oti azikhalako. Munthu wofuna kulipsirayo akamlondola komweko, anthu amumzindamo asampereke munthu wopha mnzakeyo. Koma amtchinjirize chifukwa adachita zimenezo mwangozi, pakupha Mwisraele mnzake. Sadachite zimenezo mwachiwembu. Munthuyo adzakhala mumzindamo mpaka ataweruzidwa pamaso pa anthu onse, ndiponso mpaka mkulu wa ansembe wa nthaŵi imeneyo atafa. Pamenepo munthuyo angathe kubwereranso kwao, kumudzi kumene adachoka mothaŵa kuja.’ ” Motero cha kuzambwe kwa mtsinje wa Yordani adapatula Kedesi m'dera la Galilea, m'dziko lamapiri la Nafutali. M'dziko lamapiri la Efuremu adapatula Sekemu, ndipo m'dziko lamapiri la Yuda adapatula Kiriyati-Ariba (ndiye kuti Hebroni). Kuvuma kwa Yordani, m'mapiri aja a kuvuma kwa Yeriko m'chipululu muja, adapatula Bezeri pakati pa mizinda ya fuko la Rubeni. Pakati pa mizinda ya fuko la Gadi ku Giliyadi adapatula Ramoti. Ndipo pakati pa mizinda ya fuko la Manase ku Basani adapatula Golani. Imeneyi ndiyo inali mizinda yopulumukiramo ya Aisraele onse, ngakhalenso alendo amene ankakhala pakati pao. Aliyense wopha munthu mwangozi, osati mwadala, ankatchinjirizidwa kumeneko. Womlondola kuti amlipsire sankaloledwa kumupha munthu wothaŵayo, mlandu wake usanazengedwe pamaso pa mpingo wonse. Tsiku lina atsogoleri a mabanja a fuko la Levi adabwera kwa wansembe Eleazara, kwa Yoswa, mwana wa Nuni, ndi kwa atsogoleri a mabanja a mafuko onse a Aisraele. Aleviwo adafika ku Silo m'dziko la Kanani, nanena kuti, “Chauta adalamula kudzera mwa Mose kuti ife atipatse mizinda yokhalamo, ndiponso atipatse mabusa pozungulira mizindayo, kuti tizidyetsapo zoŵeta zathu.” Motero Aisraele adapatsa Aleviwo mizindayo pochita maere, pamodzi ndi mabusa a zoŵeta, kuchokera pa magawo ao omwewo, potsata zomwe Chauta adalamula. Mabanja a Kohati ndiwo anali oyambirira kupatsidwa mizinda. Alevi amene anali zidzukulu za wansembe Aroni adapatsidwa mizinda 13, kuchokera m'mafuko a Yuda, Simeoni ndi Benjamini. Ndipo Akohati otsalawo adapatsidwa mizinda khumi kuchokera m'mafuko a Efuremu ndi Dani ndiponso theka la fuko la Manase lokhala kuzambwe kwa Yordani. Ageresoni adapatsidwa mizinda 13, kuchokera m'mafuko a Isakara, Asere, Nafutali ndi theka la fuko la Manase lokhala ku Basani. Mabanja a Merari adapatsidwa mizinda 12, kuchokera m'mafuko a Rubeni, Gadi ndi Zebuloni. Aisraele onse pamodzi adapereka mizinda imeneyi kwa Alevi mwamaere, pamodzinso ndi mabusa odyetsapo zoŵeta, potsata zomwe Chauta adaalamula kudzera mwa Mose. Mizinda ya Yuda ndi Simeoni imene idapatsidwa kwa zidzukulu za Aroni, ku banja lina limodzi la Akohati amene anali Alevi, maina ake ndi aŵa: adaŵapatsa mzinda wa Kiriyati-Ariba. (Araba anali bambo wa Anaki), dzina lake linanso ndi Hebroni. Mzindawo unali m'dziko la Yuda lamapiri lija, pamodzinso ndi mabusa a zoŵeta kuzungulira mzindawo. Komabe minda ya mzindawo pamodzi ndi midzi yake yomwe, adaipatsa Kalebe mwana wa Yefune, kuti ikhale choloŵa chake. Choncho midzi yonse imene ili m'munsimuyi, adaipatsa zidzukulu za Aroni wansembe. Poyamba Hebroni, umene unali mzinda wopulumukiramo aliyense woimbidwa mlandu wa kupha mnzake mwangozi, pamodzi ndi mabusa odyetsapo zoŵeta, ndiponso Libina, Yatiri, Esitemowa, Holoni, Debiri, Aini, Yuta ndi Betesemesi. Yonse pamodzi inalipo mizinda isanu ndi inai kuchokera m'mafuko aŵiri aja a Yuda ndi Simeoni, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta. A fuko la Benjamini adapereka Gibiyoni, Geba, Anatoti ndi Alimoni. Yonse pamodzi inalipo mizinda inai, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta. Ansembe, zidzukulu za Aroni, adapatsidwa mizinda 13, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta. Mabanja ena a Kohati, a fuko la Levi, adapatsidwa mizinda ina kuchokera ku fuko la Efuremu. Adapatsidwa Sekemu pamodzi ndi mabusa a zoŵeta. Mzindawo unali m'dziko lamapiri la Efuremu. Unalinso mzinda wopulumukiramo munthu aliyense wopha mnzake mwangozi. Adalandiranso Gezere, Kibizaimu ndi Betehoroni. Yonse pamodzi inalipo mizinda inai, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta. Kuchokera ku fuko la Dani adalandirako Elitele, Gibetoni, Ayaloni ndi Gatirimoni. Yonse pamodzi inalipo mizinda inai, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta. Kuchokera ku theka la Manase wakuzambwe adalandira mizinda iŵiri, Taanaki ndi Ibleamu, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta. Mabanja a Akohati ameneŵa adalandira mizinda khumi yonse pamodzi, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta. Ageresoni, gulu lina la fuko la Levi, adalandira mizinda iŵiri kuchokera ku theka la Manase wakuvuma: Golani ku Basani, mzinda wopulumukirapo munthu wopha mnzake mwangozi, ndi Besetera, pamodzi ndi mabusa a zoŵeta. Kuchokera ku fuko la Isakara, adalandira Kisiyoni, Daberati, Yaramuti ndi Enganimu. Yonse pamodzi inalipo mizinda inai kuphatikizapo mabusa a zoŵeta. Kuchokera ku fuko la Asere adalandira Misalu, Abidoni, Helekati ndi Rehobu. Yonse pamodzi inalipo mizinda inai, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta. Kuchokera ku fuko la Nafutali, adalandira Kedesi wa ku Galilea, mzinda wopulumukiramo aliyense wopha mnzake mwangozi, ndiponso Hamotidori ndi Karitani. Yonse pamodzi inalipo mizinda itatu, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta. Mabanja osiyanasiyana a Ageresoni adalandira mizinda khumi ndi itatu, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta. Onse otsala a fuko la Levi amene anali a m'banja la Merari, adalandira mizinda iyi kuchokera ku fuko la Zebuloni: Yokoneamu, Karita, Dimina ndi Mahalala. Yonse pamodzi inalipo mizinda inai, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta. Kuchokera ku fuko la Rubeni adalandira Bezeri, Yahazi, Kedemoti ndi Mefaati. Yonse pamodzi inalipo mizinda inai, kuphatikizapo mabusa a zoŵeta. Kuchokera ku fuko la Gadi adalandira Ramoti ku Giliyadi, mzinda wopulumukiramo munthu wopha mnzake mwangozi, ndiponso Mahanaimu, Hesiboni ndi Yazere. Yonse pamodzi inalipo mizinda inai kuphatikizapo mabusa a zoŵeta. Motero mabanja a Merari, adapatsidwa mizinda khumi ndi iŵiri mwamaere. Mizinda 48 ya m'dziko limene Aisraele adalandira idapatsidwa kwa Alevi, pamodzi ndi mabusa a zoŵeta. Mzinda uliwonse unali ndi mabusa a zoŵeta. Motero Chauta adapatsa Aisraele dziko limene Iye yemwe adaalonjeza molumbira kuti adzapatsa makolo ao. Aisraele adalandira dzikolo, nakhazikika komweko. Chauta adaŵapatsa mtendere pakati pa anthu ena onse oŵazungulira, potsata zomwe Iye adaalonjeza makolo ao. Panalibe ndi mmodzi yemwe mwa adani ao amene adatha kugonjetsa Aisraele, chifukwa choti Chauta adaŵapatsa mphamvu zopambanira adani ao. Zoonadi Chauta adasunga malonjezo onse amene adaachita ndi Aisraele. Pambuyo pake Yoswa adaitana anthu a fuko la Rubeni ndi la Gadi, ndi hafu lina lija la fuko la Manase wakuvuma. Ndipo adaŵauza kuti, “Zonse zimene Mose mtumiki wa Chauta adakulamulani kuti muchite, mwachitadi, ndipo mwamvera malamulo anga onse. Aisraele anzanu simudaŵasiye nthaŵi yonseyi mpaka lero lino. Mwasamaladi malamulo onse a Chauta, Mulungu wanu. Tsopano Chauta, Mulungu wanu, wapatsa mtendere Aisraele anzanu, monga momwe adaalonjezera. Motero bwererani kwanu ku dziko limene mudalandira, dziko limene lili patsidya pa mtsinje wa Yordani kuvuma, limene Mose mtumiki wa Chauta adakupatsani. Musamale bwino kuti mumvere ndithu malamulo ndi malangizo amene Mose mtumiki wa Mulungu adakupatsani. Muzikonda Chauta, Mulungu wanu, muzichita zimene Iyeyo akufuna, muzimvera malamulo ake, muzikhala okhulupirika kwa Iye, ndipo muzimtumikira ndi mtima wanu wonse ndi mzimu wanu wonse.” Kenaka Yoswa adaŵadalitsa anthuwo, naŵauza kuti apite. Tsono anthuwo adapita kwao. Mose anali atapatsa theka lina la fuko la Manase ku dziko la Basani. Koma theka lina la fuko la Manase, Yoswa adalipatsa dziko kuzambwe kwa Yordani, pamodzi ndi abale ao onse. Pamene Yoswa ankaŵatumiza kwao anthu amenewo, adaŵadalitsa, naŵauza kuti, “Tsopano mukubwerera kwanu mutalemera. Muli ndi ng'ombe zambiri, mulinso ndi siliva, golide, mkuŵa, zitsulo ndi zovala zambiri. Izi zimene mudafunkha kwa adani anu, mugaŵireko Aisraele anzanu.” Motero anthu onse a fuko la Rubeni ndi la Gadi, pamodzi ndi theka lija la fuko la Manase, adabwerera kwao. Aisraele ena onse adaŵasiya ku Silo m'dziko la Kanani, ndipo iwowo adapita ku dziko la Giliyadi. Dziko limeneli ndilo linali lao, chifukwa adalilandira potsata malamulo a Chauta kudzera mwa Mose. Anthuwo atafika ku Geliloti, malo omwe anali pambali pa mtsinje wa Yordani m'dziko la Kanani, adamangako guwa lalikulu ndi lokoma pambali pa mtsinjewo. Tsono Aisraele ena onse adauzidwa kuti, “Tamvani! Anthu onse a fuko la Rubeni ndi la Gadi, pamodzi ndi theka lija la fuko la Manase adamanga guwa ku Geliloti m'malire a dziko la Kanani, tsidya lakuno la Yordani, moyang'anana ndi Israele.” Tsono Aisraele atamva zimenezi, onse pamodzi adasonkhana ku Silo, kuti apite kukamenyana nawo nkhondo. Pomwepo Aisraelewo adatuma Finehasi, mwana wa wansembe Eleazara kwa anthu a fuko la Rubeni ndi la Gadi ndiponso a theka lina lija la Manase, amene ankakhala ku dziko la Giliyadi. Finehasiyo adapita pamodzi ndi akuluakulu khumi ochokera ku fuko lililonse la Aisraele. Aliyense mwa akuluakulu amenewo anali mtsogoleri wa banja limodzi la mafukowo. Adafika ku dziko la Giliyadi, naŵauza anthu a fuko la Rubeni, la Gadi ndi theka lina lija la fuko la Manase kuti, “Anthu onse a Chauta alikufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani inu mwachimwa chotere, potsutsana ndi Mulungu wa Israele? Mwapandukira Chauta ndi kutsutsana naye pakudzimangira guwa limeneli, ndipo simukumtsatanso. Kumbukirani tchimo la ku Peori lija limene Chauta adalanga nalo anthu ake poŵatumizira mliri woopsa. Mpaka lero lino, tchimo limene lija tidakasauka nalobe. Kodi tchimo limene lija ndi lochepa? Kodi tsopano mufuna kuleka kutsata Chauta, Mulungu wanu? Mukampandukira lero lino, Iye adzakwiyira mtundu wonse wa Aisraele maŵamaŵali. Motero tsono, ngati dziko lanulo ndi losayenera kupembedzeramo, pitani uko ku dziko la Chauta komwe kuli chihema chake chija, ndipo mugaŵane nafe dziko lathulo. Koma musapikisane ndi Chauta kapena kutisandutsanso ochimwa ife, podzimangira guwa lina kulimbana ndi Chauta, Mulungu wathu. Kumbukirani kuti Akani, mwana wa Zera uja, adakana kumvera lamulo la zinthu zoyenera kuwonongedwa zija, ndipo Aisraele onse adalangidwa. Akaniyo sadafe yekha chifukwa cha tchimo lakelo.’ ” Pamenepo fuko la Rubeni, ndi la Gadi pamodzi ndi theka lina lija la fuko la Manase, adayankha atsogoleri a mabanja a Aisraelewo kuti, “Wamphamvu uja, Mulungu, Iyeyo ndiye Chauta. Wamphamvu uja, Mulungu, Iyeyo ndiye Chauta. Akudziŵa chifukwa chake chimene tidachitira zimenezi, ndipo inunso muyenera kudziŵa. Ngati tidapanduka ndi kuleka kukhulupirira Chauta, musatilole kukhalanso ndi moyo. Ngati sitidamvere Chauta pamene tidadzimangira tokha guwa lopserezapo nsembe, kapena kumapereka zopereka zatirigu kapena zopereka zamtendere, Chauta yekha ndiye atilange. Tidachita zimenezi chifukwa choopa kuti kutsogoloko zidzukulu zanu zingamadzanene zidzukulu zathu kuti, ‘Chauta, Mulungu wa Aisraele, kodi inu muli naye nkanthu? Chauta adaika malire a Yordani pakati pa ife ndi inu, anthu a fuko la Rubeni ndi Gadi. Motero, inu mulibe gawo mwa Chauta.’ Tsono mwina zidzukulu zanuzo nkudzaletsa zidzukulu zathu kupembedza Chauta. Nchifukwa chake tidamanga guwa, osati kuti tizipserezapo nsembe kapena kumapereka zopereka pamenepo, koma makamaka kuti chikhale chizindikiro pakati pa ife ndi inu. Ndipo chikhalenso chizindikiro kwa mibadwo yobwera pambuyo pathu, kuti idzadziŵe kuti timapembedzanso Chauta ndi nsembe zathu zopsereza, zopereka, ndiponso nsembe zamtendere. Motero zidzukulu zanu zisadzanene kwa zidzukulu zathu m'tsogolo muno kuti, ‘Inu mulibe gawo mwa Chauta.’ Ameneŵa ndiwo anali maganizo athu kuti, ngati zimenezi zidzachitika, ife tidzanene kuti, ‘Onani, makolo athu adamanga guwa lofanafana ndi guwa la Chauta. Limeneli silinali loperekerapo nsembe zopsereza kapena lopherapo nyama za nsembe, koma linali chizindikiro pakati pa ife ndi inu.’ Sitingathe kupandukira Chauta. Sitingathenso kuleka kumtsata tsopano lino, ndi kumanga guwa la zopereka zopsereza, kapena chopereka cha chakudya kapenanso la nsembe zina, loti lizipikisana ndi guwa la Chauta wathu lomwe lili patsogolo pa malo opatulika m'mene Chauta amakhalamo.” Wansembe Finehasi ndi akuluakulu amene anali naye, amene anali atsogoleri a mabanja a Aisraele, atamva zimene adanena anthu a fuko la Rubeni ndi la Gadi ndi la Manase, adakondwa kwambiri. Ndipo Finehasi, mwana wa wansembe Eleazara, adauza anthu a mafuko aja kuti, “Tsopano tadziŵadi kuti Chauta ali nafe, poti simudapanduke ndi kutsutsana ndi Chauta. Mwapulumutsa Aisraele ku chilango cha Chauta.” Tsono Finehasi, pamodzi ndi mafumuwo adachoka ku Giliyadi nasiya anthu a fuko la Rubeni pamodzi ndi la Gadi, nabwerera ku Kanani kwa Aisraele anzao, ndipo adakafotokoza zonsezo. Mau adafotokozawo adakondwetsa Aisraele onse. Adatamanda Mulungu, ndipo sadakambenso za nkhondo yokaononga dziko limene anthu a mafuko a Rubeni ndi Gadi ankakhalamo. Choncho anthu a mafuko a Rubeni ndi Gadi adalitcha guwalo kuti Mboni, chifukwa iwowo adati, “Chimenechi ndi mboni kwa tonsefe kuti Chauta ndi Mulungudi.” Padapita nthaŵi yaikulu chiyambire pamene Chauta adakhazikitsa mtendere pakati pa Aisraele ndi adani ao oŵazungulira. Pamenepo nkuti Yoswa atatheratu nkukalamba. Tsono Yoswayo adaitana Aisraele onse, pamodzi ndi akuluakulu, atsogoleri, aweruzi ndi akapitao a anthuwo, naŵauza kuti “Tsopano ine ndakalamba. Zonse zimene Chauta wachitira mitundu ina yonseyi chifukwa cha inu, mwazipenya. Chauta, Mulungu wanu, ndiye amene wakumenyerani nkhondo. Tamvani tsono, mitundu imene simudaipambanebe, ndaipereka kwa mafuko anu, chimodzimodzi mitundu inayo imene ndidaiwononga pakati pa Yordani ndi Nyanja Yaikulu kuzambweko. Chauta, Mulungu wanu, ndiye amene adzaŵathaŵitse pamaso panu. Inuyo mudzatenga maiko ao monga momwe Chauta, Mulungu wanu, wakulonjezerani. Motero, muchenjere kuti mumvere ndi kumachitadi zonse zomwe zidalembedwa m'buku la malamulo a Mose. Musanyozere gawo lina lililonse la malamulowo, ndipo musagwirizane ndi anthu aŵa amene atsala pakati panu. Musamatchula maina a milungu yao kapena kulumbira poitchula, kapena kumaitumikira, kapenanso kumaigwadira. Mukamakhulupirira Chauta, monga momwe mwachitira mpaka tsopano lino, Chauta adzakupirikitsirani mitundu yaikuluikulu ndi yamphamvu. Mpaka pano, palibe ndi mmodzi yemwe wotha kulimbana nanu. Aliyense mwa inu angathe kuthamangitsa anthu chikwi chimodzi, chifukwa Chauta ndiye akukumenyerani nkhondo monga adalonjezera. Musamale kwambiri tsono kuti mukonde Chauta, Mulungu wanu. Mukabwerera m'mbuyo ndi kuphatikizana ndi mitundu yotsalira ili pakati panuyi, ndi kumakwatirana nayo, pamenepo mudziŵe kuti Chauta, Mulungu wanu, sadzapirikitsa mitundu imeneyi pamaso panu. Koma anthuwo adzakhala ngati msampha kwa inu, kapenanso ngati khwekhwe. Adzakhalanso ngati chikoti choŵaŵa pamsana panu, kapena ngati minga zokulasani m'maso mwanu. Zimenezi zidzachitikabe mpaka inuyo mutatha m'dziko labwinoli limene Chauta, Mulungu wanu, wakupatsani. “Ine ndi ulendo uno tsopano. Aliyense mwa inu akudziŵa bwino lomwe mumtima mwake ndi mumzimu mwake kuti Chauta, Mulungu wanu, wakupatsani zinthu zonse zabwino zimene adaalonjeza. Zonse zimene adaalonjeza, zachitika. Palibe lonjezo ndi limodzi lomwe limene silidachitike. Monga momwe Chauta, Mulungu wanu, wakuchitirani zabwino zonse zimene adaanena kuti adzachita, choncho angathe kukuchitani zoipa, mpaka kukuchotsani m'dziko lokomali limene Iye adakupatsani. Ngati simusunga chipangano chomwe Chauta adakulamulani, mukamapita kukatumikira milungu ina ndi kumakaigwadira, Chauta adzakupserani mtima, ndipo sipadzatsala ndi mmodzi yense m'dziko labwino limene adakupatsanilo.” Tsono Yoswa adasonkhanitsa mafuko onse a Aisraele ku Sekemu. Adaitana akuluakulu, atsogoleri, aweruzi ndi akapitao a Aisraele, ndipo onsewo adafika pamaso pa Mulungu. Adauza anthu onsewo kuti, “Zimene Chauta, Mulungu wa Aisraele, akunena ndi izi, akuti, ‘Kale makolo anu ankakhala pa mbali ina ya mtsinje wa Yufurate, ndi kumapembedza milungu ina. Mmodzi mwa makolo ameneŵa anali Tera, bambo wa Abrahamu ndi Nahori. Tsono Abrahamuyo ndidamtenga ndi kumchotsa m'dzikomo patsidya pa Yufurate, ndipo ndidamtsogoza kupita naye ku dziko la Kanani. Ndidampatsa zidzukulu zambiri. Ndidampatsa Isaki, ndipo Isakiyo ndidampatsa Yakobe ndi Esau. Dziko lamapiri la Seiri ndidapatsa Esau kuti likhale choloŵa chake, koma Yakobe ndi ana ake adatsikira ku Ejipito. Pamenepo ndidatuma Mose ndi Aroni ku Ejipitoko, ndipo ndidazunza kwambiri Aejipitowo. Pambuyo pake ndidakutulutsani inu. Nditatulutsa makolo anu ku dziko la Ejipito, ndidafika nawo ku Nyanja Yofiira, koma Aejipito okwera pa magaleta ndi pa akavalo adaŵatsatira mpaka kunyanjako. Makolo anuwo atapemphera mokhulupirira kwa Ine, ndidaika mtambo wakuda pakati pa iwo ndi Aejipitowo, ndipo nyanja idaŵamiza Aejipito onsewo. Mudapenya ndi maso anu zomwe ndidachita Ejipito, ndipo mudakhala nthaŵi yaitali m'chipululu. “ ‘Pambuyo pake Ine ndidakufikitsani ku dziko la Aamori, amene ankakhala kuvuma kwa mtsinje wa Yordani. Adalimbana nanu iwowo, koma Ine ndidaŵapereka m'manja mwanu, mwakuti mudalanda dziko lao, chifukwa Ine ndidaŵaononga inu mukufika. Tsono Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Amowabu, adalimbana ndi Israele. Iyeyu adatumiza mau kwa Balamu mwana wa Beori, nampempha kuti akutemberereni. Koma Ine sindidamvere Balamuyo, motero iyeyo adakudalitsani, ndipo ndidakupulumutsani m'manja mwa Balaki. Mudaoloka Yordani ndi kufika ku Yeriko. Anthu a ku Yeriko adalimbana nanu, kudzanso Aamori, Aperizi, Akanani, Ahiti, Agirigasi, Ahivi ndi Ayebusi. Ine ndidaŵapereka m'manja mwanu. Ndine amene ndidatumiza zoluma zija kuti zizunze mafumu a Aamori aja, ndipo onsewo adapirikitsidwa pamaso panu. Si malupanga kapena mauta anu amene adachititsa zimenezi ai. Ndidakupatsani dziko limene inuyo simudaligwirire ntchito, pamodzi ndi mizinda imene simudaimange. Mukukhala kumeneko ndi kumangodya mphesa ndi olivi, zimene inu simudabzale.’ “Tsono inu, opani Chauta ndipo mumtumikire moona ndi mokhulupirika. Chotsani milungu imene makolo anu ankaipembedza pambali pa mtsinje wa Yufurate ndi ku Ejipito, ndipo mutumikire Chauta. Ngati simufuna kutumikira Chauta, sankhani lero lomwe lino amene muti mudzamtumikire, kapena ndi milungu ya Aamori amene mukukhala nawo m'dziko mwao. Koma ine pamodzi ndi banja langa lonse, tidzatumikira Chauta.” Apo anthuwo adayankha kuti, “Zoti nkusiya Chauta ndi kumakatumikira milungu ina ndiye ai, ife sitingathe kuchita zotere mpang'ono pomwe. Chauta, Mulungu wathu, ndiye amene adatulutsa makolo athu pamodzi ndi ife tomwe mu ukapolo, ku dziko la Ejipito. Ndipo tidaonanso ndi maso athu zinthu zazikulu zimene adachita. Ife tikufika, Chauta ankapirikitsa Aamori amene ankakhala m'dziko lino. Motero nafenso tidzatumikira Chauta, chifukwa ndiye Mulungu wathu.” Pamenepo Yoswa adauza anthuwo kuti, “Mwina mwaketu inu simungathe kutumikira Chauta chifukwa ndi Mulungu woyera, wosalola kupikisana naye. Ndipo sadzakulekererani mukumpandukira ndi kumamchimwira. Mukasiya Chauta, Mulungu wanu, ndi kumakatumikiranso milungu yachilendo, adzakufulatirani, ndipo adzakulangani. Adzakuwonongani ngakhale kuti kale adakuchitirani zabwino.” Ndipo anthuwo adauza Yoswa, kuti, “Iyai! Ife tidzatumikira Chauta.” Tsono Yoswa adaŵauza kuti, “Inu mukudzichitira nokha umboni kuti mwasankhula kutumikira Chauta.” Anthuwo adavomera kuti, “Inde, mboni ndife tomwe.” Yoswa adatinso, “Chotsani milungu yachilendo imene ili pakati panu, ndipo muzipembedza Chauta, Mulungu wa Israele, mokhulupirika.” Anthuwo adauza Yoswa kuti, “Tidzatumikira Chauta, Mulungu wathu, ndipo tidzamvera malamulo ake.” Motero Yoswa adapangana nawo anthu pa tsiku limenelo, ndipo ku Sekemu komweko Yoswa adapatsa anthuwo malamulo ndi malangizo. Yoswayo adalemba malamulo ameneŵa m'buku la malamulo a Mulungu, ndipo adatenga chimwala chachikulu nachiimiritsa patsinde pa mtengo wa thundu pa malo opatulika a Chauta. Ndipo adauza anthuwo kuti, “Mwala umenewu udzakhala mboni yotitsutsa. Mau amene Chauta walankhula ndi ifeŵa, mwalawu wamva. Motero udzakhala mboni yokutsutsani, ngati mudzakane Mulungu wanu.” Tsono Yoswa adaŵalola anthuwo kuti aliyense abwerere ku dziko lake. Zitatha zimenezi, Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Chauta, adamwalira. Anali ndi zaka 110 zakubadwa. Adamuika m'dziko lake ku Timnati-Sera, m'dziko lamapiri la Efuremu, kumpoto kwa phiri la Gasi. Aisraele adatumikira Chauta pa nthaŵi yonse ya moyo wa Yoswa ndiponso pa nthaŵi ya atsogoleri amene adakhala ndi moyo Yoswa atafa. Atsogoleriwo adadziŵa ntchito zonse zimene Chauta adachitira Israele. Mafupa a Yosefe amene Aisraele adaŵatenga ku Ejipito, adakaŵaika ku Sekemu m'kadziko kamene Yakobe adaagula kwa ana a Hamori, bambo wa Sekemu, pa mtengo wa ndalama zasiliva zana limodzi. Ndipo dzikolo lidasanduka choloŵa cha zidzukulu za Yosefe. Eleazara, mwana wa Aroni, nayenso adamwalira, ndipo adamuika ku Gibea m'mudzi wa mwana wake Finehasi, umene adaamupatsa m'dziko lamapiri la Efuremu. Yoswa atafa, Aisraele adafunsa Chauta kuti, “Ndani mwa ife amene ayambe kulimbana ndi Akanani, kumenyana nawo nkhondo?” Chauta adayankha kuti, “Fuko la Yuda ndilo limene lipite. Ndikuŵapatsa dzikolo m'manja mwao.” Pamenepo Ayuda adauza abale ao, anthu a fuko la Simeoni, kuti, “Tiyeni tipite limodzi m'dziko limene Chauta adagaŵira ife, kuti tikamenyane ndi Akanani. Pambuyo pake nafenso tidzapita nanu limodzi m'dziko limene adagaŵira inu.” Choncho Asimeoni adatsakana nawo. Onsewo adapita, ndipo Chauta adapereka Akananiwo m'manja mwao pamodzi ndi Aperizi omwe. Ndipo adagonjetsa anthu 10,000 ku Bezeki. Kumeneko Ayuda adakumana ndi ankhondo a mfumu Adonibezeki, ndipo adamenyana nawo; adaŵagonjetsa Akanani ndi Aperizi omwe. Adonibezekiyo adathaŵa, koma adamthamangira namgwira, ndipo adadula zala zake zazikulu zakumanja ndiponso zala zake zazikulu zakumwendo. Apo Adonibezeki adati, “Mafumu makumi asanu ndi aŵiri oduka zala zazikulu zakumanja ndi zakumwendo ankatola nyenyeswa pansi pa tebulo langa. Mulungu wandichita zomwe ndidaŵachita iwowo.” Anthu ake adapita naye ku Yerusalemu ndipo iye adafera komweko. Pambuyo pake Ayuda adathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu, naulanda. Adapha anthu ambiri, natentha mzinda wonsewo ndi moto. Kenaka Ayudawo adapita kukamenyana ndi Akanani amene ankakhala m'dziko lamapiri, m'dziko la Negebu lakumwera, ndiponso m'zigwa. Adakalimbananso ndi Akanani amene ankakhala ku Hebroni, (mzinda umene kale ankautchula kuti Kiriyati-Ariba). Kumeneko adagonjetsa mabanja a Sesai, Ahimani ndiponso Talimai. Kuchokera kumeneko anthu a ku Yuda aja adapita kukalimbana ndi anthu a ku Debiri. Mzinda umenewu kale unkatchedwa Kiriyati-Sefere. Tsono Kalebe adati, “Mkulu wa ankhondo amene athire nkhondo mzinda wa Kiriyati-Sefere, naulanda, ndidzampatsa mwana wanga Akisa kuti akhale mkazi wake.” Mng'ono wake wa Kalebe, Otiniyele, mwana wa Kenazi, adaulanda mzindawo. Choncho Kalebe adampatsa mwana wake Akisa kuti akhale mkazi wake. Tsiku lina, Akisayo atafika, Otiniyele adamuumiriza mkazi wakeyo kuti apemphe munda kwa Kalebe bambo wake. Tsono Akisa atatsika pa bulu wake, Kalebe adamufunsa kuti, “Kodi ukufuna kanthu?” Iye adayankha kuti, “Ndimati mundipatseko mphatso. Popeza kuti mwandikhazika m'dziko la Negebu lopanda madzi, mundipatsenso akasupe a madzi.” Pamenepo Kalebe adampatsa akasupe akumtunda ndi akuchigwa omwe. Tsono zidzukulu za Mkeni uja, mpongozi wa Mose, zidapita nawo limodzi anthu a fuko la Yuda kuchokera ku mzinda wamigwalangwa mpaka ku chipululu chimene chili kumwera kwa Aradi, m'dziko la Yuda. Kumeneko adakakhala ndi Aamaleke. Ayuda adatsakana ndi abale ao Asimeoni ndipo adagonjetsa Akanani amene ankakhala mu mzinda wa Zefati, naononga mzindawo kwathunthu. Choncho mzindawo adautcha Horima. Ayuda adalandanso mzinda wa Gaza ndi dziko lake lonse lozungulira, Asikeloni ndi dziko lake lonse lozungulira, ndiponso Ekeroni ndi dziko lake lonse lozungulira. Chauta adaŵathandiza Ayuda, ndipo Ayudawo adalanda dziko lamapiri, koma sadathe kupirikitsa nzika zam'chigwa, chifukwa chakuti zinali ndi magaleta achitsulo. Mzinda wa Hebroni udapatsidwa kwa Kalebe, monga adaanenera Mose. Ndipo Kalebeyo adapirikitsa mafuko atatu a Anaki mumzindamo. Koma Abenjamini sadapirikitse Ayebusi amene ankakhala mu Yerusalemu. Choncho Ayebusi akukhala nawobe Abenjamini mu Yerusalemu mpaka pano. Mafuko a Yosefe nawonso adapita kukalimbana ndi mzinda wa Betele, ndipo Chauta anali nawo iwowo. Adatuma anthu oti akazonde Betele, (mzinda umene kale ankautchula Luzi). Anthu ozondawo adaona munthu akutuluka mumzindamo namuuza kuti, “Chonde tatidziŵitsaniko njira yoloŵera mumzindamu, ife tikuchitirani zabwino.” Munthuyo adaŵasonyeza njira yoloŵera mumzindamo. Iwo aja adapha anthu onse amumzindamo ndi lupanga, koma munthu uja adamleka osamupha, pamodzi ndi banja lake. Munthuyo adapita ku dziko la Ahiti nakamangako mzinda nkuutcha dzina loti Luzi. Limenelo ndilo dzina lake mpaka pano. Koma a fuko la Manase sadapirikitse nzika za mu Beteseani ndi za m'midzi yake yozungulira, kapenanso nzika za mu Taanaki ndi za m'midzi yake yozungulira. Sadapirikitsenso nzika za mu Dori ndi za m'midzi yake yozungulira, kapenanso nzika za mu Ibleamu ndi za m'midzi yake yozungulira. Nazonso nzika za mu Megido ndi za m'midzi yake yozungulira sadazipirikitse. Choncho Akanani adapitirirabe kukhala m'dzikomo. Pamene Aisraele adasanduka amphamvu, adayamba kuŵagwiritsa Akananiwo ntchito yaukapolo, koma sadaŵapirikitse. Aefuremu sadapirikitse Akanani amene ankakhala mu Gezere. Choncho Akananiwo ankakhala pakati pao ku Gezereko. Azebuloni sadapirikitse nzika za mu Kitironi ndi nzika za mu Nahaloli. Choncho Akananiwo ankakhala pakati pao nasanduka oŵagwirira ntchito yaukapolo. Aasere sadapirikitse nzika za mu Ako, nzika za mu Sidoni, nzika za mu Alabu, nzika za mu Akizibu, nzika za mu Heliba, nzika za mu Afiki ndiponso nzika za mu Rehobu. Koma Aasere adakhala pakati pa Akanani, nzika za dzikolo, pakuti sadaŵapirikitse Akananiwo. Anafutali sadapirikitse nzika za mu Betesemesi ndi nzika za mu Betanati, koma ankakhala pakati pa Akananiwo, nzika za dzikolo. Komabe nzika za mu Betesemesi ndi za mu Betanati ankazigwiritsa ntchito yaukapolo. Aamori adapirikitsira anthu a fuko la Dani ku dziko lamapiri ndipo sadaŵalole kuti atsikire ku zigwa. Aamori sadachoke koma ankakhalabe ku phiri la Heresi, ku Aiyaloni, ndiponso ku Salibimu. Koma a fuko la Yosefe adasanduka amphamvu, nagwiritsa Aamoriwo ntchito yaukapolo. Tsono malire a Aamori adayambira ku chikwera cha Akirabimu, nkuloŵera ku Sela, napitirira kumapita chakumapiri ndithu. Mngelo wa Chauta adapita ku Bokimu kuchokera ku Giligala. Ndipo adauza Aisraele kuti, “Ndidakutulutsani ku Ejipito ndi kukuloŵetsani m'dziko limene ndidalumbira kuti ndidzapatsa makolo anu. Ndidati, ‘Ineyo sindidzaswa konse chipangano changa ndi inu. Tsono inuyo musadzachite chipangano ndi nzika za dziko lino. Mudzaphwanye maguwa ao onse.’ Koma inu simudamvere lamulo langa. Zimenezi mwachitiranji? Choncho tsopano ndikukuuzani kuti sindidzapirikitsa nzikazo pamene inu mukufika. Koma zidzasanduka adani anu, ndipo milungu yao idzakhala ngati msampha kwa inu.” Pamene mngelo wa Chauta adalankhula mau ameneŵa kwa Aisraele onse, anthuwo adayamba kufuula ndi kulira. Malowo adaŵatcha Bokimu (ndiye kuti olira), ndipo adapereka nsembe kwa Chauta pomwepo. Yoswa atauza anthu kuti apite, Aisraele adapita aliyense ku dera la choloŵa chake, kuti akhazikike konko. Anthuwo ankatumikira Chauta masiku onse pamene Yoswa anali moyo, ndipo ngakhale atafa Yoswayo, anthu ankatumikirabe Chauta nthaŵi yonse ya moyo wa akuluakulu otsatira Yoswa aja, amene anali ataona ntchito zazikulu zimene Chauta adachitira Aisraele. Yoswa, mwana wa Nuni, mtumiki wa Chauta, adamwalira ali ndi zaka 110. Ndipo adamuika m'dziko lake limene adalandira ngati choloŵa chake ku Timnati-Heresi m'dziko lamapiri la Efuremu, kumpoto kwa phiri la Gaasi. Mbadwo wonsewo udafa. Tsono padauka mbadwo wina pambuyo pake umene sudadziŵe Chauta kapenanso ntchito zija Chauta adaachitira Aisraelezi. Aisraele adayamba kuchita zinthu zoipira Chauta nkumatumikira Baala. Iwo adasiya Chauta, Mulungu wa makolo ao, amene adaŵatulutsa m'dziko la Aejipito. Adatsata milungu ina ya anthu oŵazungulira, ndipo ankaipembedza. Pakutero adakwiyitsa Chauta. Iwo adasiya Chauta, nayamba kutumikira Abaala ndi Aasitaroti. Choncho Chauta adaŵapsera mtima Aisraelewo, ndipo adaŵapereka m'manja mwa anthu ofunkha amene adasakaza zinthu zao. Ndipo adalola kuti adani ao oŵazungulira aŵagonjetse, kotero kuti sadathenso kulimbana nawo adaniwo. Ankati akapita kukamenya nkhondo, Chauta ankalimbana nawo iwowo, monga momwe Iye adaanenera molumbira kuti adzaterodi. Choncho Aisraelewo anali pa mavuto oopsa. Tsono Chauta adautsa atsogoleri amene adaŵapulumutsa Aisraele kwa anthu osakaza aja amene ankaŵaonongera zinthu zao. Komabe iwo sadaŵamvere atsogoleri aowo, pakuti ankapembedza milungu ina namaigwadira. Makolo ao ankamvera malamulo a Chauta. Koma mbadwo watsopanowu udaleka mwamsanga kutsata njira imeneyo. Nthaŵi zonse Chauta akaŵautsira mtsogoleri, Chauta ankakhala naye, ndipo mtsogoleriyo ankaŵapulumutsa Aisraele kwa adani ao nthaŵi zonse mtsogoleriyo ali moyo. Zoonadi Chauta ankaŵamvera chisoni anthuwo, iwowo akamamdandaulira chifukwa cha amene ankaŵazunza ndi kuŵasautsa. Koma nthaŵi zonse mtsogoleri akafa, anthuwo ankayambanso kuchita zoipa, nkusanduka oipa kupambana makolo ao, namatsata milungu ina, kumaitumikira ndi kumaigwadira. Sankaleka kuchita zimene adaazoloŵera ndiponso sankaleka kukhala ouma mitu. Choncho Chauta adaŵapsera mtima Aisraele, nati, “Anthuŵa aphwanya chipangano changa chimene ndidaakhazikitsira makolo ao. Ndiye popeza kuti sadamvere mau anga, kuyambira tsopano sindidzapirikitsanso mtundu wina uliwonse umene Yoswa adasiya pamene ankamwalira. Motero ndidzaŵayesa Aisraele kuti ndiwone ngati adzasamala zoyenda m'njira ya Ine Chauta, monga adachitira makolo ao, kapena ai.” Choncho Chauta adaisiya mitundu imeneyo osaipirikitsa nthaŵi yomweyo, ndipo sadaipereke m'manja mwa Yoswa. Tsono Chauta adasiya mitundu ina ya anthu, kuti ayese nayo Aisraele, ndiye kuti Aisraele onse amene sadamenye nao nkhondo ku Kanani. Chauta ankangofuna kuti mibadwo yonse ya Aisraele idziŵe kumenya nkhondo, ndiponso kuti aphunzitse makamaka amene sadaidziŵe nkhondo nkale lonse. Mitunduyo ndi iyi: mafumu asanu a Afilisti, Akanani onse, Asidoni onse ndi Ahivi amene ankakhala ku mapiri a Lebanoni, kuyambira ku phiri la Baala-Heremoni mpaka ku mpata wa Hamati. Adaŵasiya kuti aziyesa nawo Aisraele, kuti aone ngati Aisraele adzamvera malamulo amene Chauta adaapatsa makolo ao kudzera mwa Mose. Choncho Aisraele adakhala pakati pa Akanani, Ahiti, Aamori, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi. Aisraelewo adayamba kukwatirana ndi anthu a mitundu imeneyo, ndiponso kukwatitsa ana ao kwa amuna a mitundu inayo. Kenaka adayamba kupembedza milungu yao. Aisraele adachita zinthu zoipira Chauta. Adaiŵala Chauta, Mulungu wao, namatumikira mafano a Abaala ndi Asitaroti. Nchifukwa chake Chauta adaŵapsera mtima Aisraelewo, naŵagulitsa kwa Kusani-Risataimu mfumu ya ku Mesopotamiya. Choncho Aisraele adatumikira Kusani-Risataimu zaka zisanu ndi zitatu. Koma pamene Aisraele adalira kwa Chauta, Chautayo adaŵautsira munthu woŵapulumutsa; amene adaŵapulumutsayo ndi Otiniyele, mwana wa Kenazi, mng'ono wake wa Kalebe. Mzimu wa Chauta udatsika pa iye, ndipo adasanduka mtsogoleri wa Aisraele. Adapita kukamenya nkhondo, ndipo Chauta adapereka Kusani-Risataimu, mfumu ya ku Mesopotamiya, m'manja mwake, namgonjetsa. Motero dziko lidakhala pa mtendere zaka makumi anai. Pambuyo pake Otiniyele, mwana wa Kenazi, adamwalira. Aisraele adachitanso zinthu zoipira Chauta. Ndiye Chauta adapatsa mphamvu Egiloni, mfumu ya ku Mowabu, kuti alimbane ndi Aisraele, chifukwa chakuti iwowo adaachita zinthu zoipira Chauta. Egiloniyo adamemeza Aamoni ndiponso Aamaleke, napita kukagonjetsa Aisraele. Ndipo adalanda Yeriko, mzinda wamigwalangwa. Tsono Aisraele adakhala akapolo a Egiloni, mfumu ya ku Mowabu, zaka 18. Koma pamene Aisraele adalira kwa Chauta, Chautayo adaŵautsira munthu woŵapulumutsa. Iyeyu anali Ehudi, mwana wa Gera, wa fuko la Benjamini, munthu wamanzere. Aisraele ankatumiza msonkho kwa Egiloni, mfumu ya ku Mowabu, kudzera kwa Ehudi. Tsono Ehudi adasula lupanga lake lakuthwa kuŵiri, kutalika kwake masentimita 50. Ndipo adamangirira lupangalo pa ntchafu yake yakumanja m'kati mwa zovala zake. Adapita kukapereka msonkho kwa Egiloni, mfumu ya ku Mowabu, amene anali wonenepa kwambiri. Ehudi atamaliza kupereka msonkhowo, adauza anthu onyamula msonkhowo kuti azipita. Koma iyeyo adabwerera pa malo a miyala yozokotedwa ku Giligala, ndipo atafika kwa mfumu adati, “Zikomo amfumu, ndimati ndikuuzeni mau achinsinsi.” Pamenepo mfumuyo idalamula atumiki ake kuti akhale chete, niŵatulutsa onsewo. Tsono Ehudi adasendera pafupi ndi mfumuyo, iyoyo itakhala yokhayokha m'chipinda cham'mwamba chozizira bwino. Ndipo adati, “Ndili ndi mau ochokera kwa Mulungu oti ndikuuzeni.” Mfumuyo idadzuka pa mpando wake. Apo Ehudi ndi dzanja lake lamanzere, adasolola lupanga pa ntchafu yake yakumanja ndi kubaya nalo mfumuyo pa mimba. Lupangalo lidaloŵa ndi chigumbu chomwe, ndipo mafuta adaphimba lupangalo pakuti sadalitulutsenso m'mimbamo, adalisiya litatulukira kumbuyo. Ehudi adatulukira m'khonde, atatseka ndi kukhoma zitseko za chipinda cham'mwambacho. Ehudi atachoka, atumiki a mfumu adabwera. Ataona kuti zitseko za chipinda cham'mwamba nzokhoma, adaganiza kuti, “Kapena mfumu ikudzithandiza m'katimo.” Iwo adadikira nthaŵi yaitali, kotero kuti sadaone konse chochita. Koma ataona kuti mfumuyo sidatsekulebe zitseko zija, adatenga kii natsekula zitsekozo, ndipo adangoona mfumu yao ili thasa pansi, itafa. Ehudi adathaŵa pamene iwo ankachedwa nkudikira. Adapitirira malo a miyala yozokota ija, nathaŵira ku Seira. Atangofika adaimba lipenga m'dziko lamapiri la ku Efuremu. Aisraele onse adatsika pamodzi naye kuchokera ku dziko lamapirilo, iyeyo akuŵatsogolera. Adauza anthuwo kuti, “Tiyeni kuno, Chauta wapereka Amowabu, adani anu, m'manja mwanu.” Choncho anthuwo adamtsata nakalanda madooko a Yordani natsekereza Amowabuwo, osalola kuti munthu ndi mmodzi yemwe aoloke. Nthaŵi imeneyo adapha Amowabu pafupi 10,000. Anthu onse ophedwawo anali amphamvu ndiponso odziŵa kumenya nkhondo, koma sadapulumukepo ndi mmodzi yemwe. Choncho Amowabu adagonjetsedwa ndi Aisraele pa tsiku limenelo. Ndipo dzikolo lidakhala pa mtendere zaka makumi asanu ndi atatu. Atamwalira Ehudi, padabwera Samigara, mwana wa Anati, amene adapha Afilisti 600 ndi ndodo yomenyera ng'ombe. Motero iyeyunso adapulumutsa Aisraele. Ehudi atamwalira, Aisraele adachitanso zinthu zoipira Chauta. Ndipo Chauta adaŵapereka m'manja mwa Yabini, mfumu ya ku Kanani, amene ankalamulira ku Hazori. Mtsogoleri wa ankhondo ake anali Sisera amene ankakhala ku Haroseti-Goimu. Tsono Aisraele adalira kwa Chauta kuti aŵathandize, pakuti Sisera anali ndi magaleta achitsulo okwanira 900, ndipo adaazunza Aisraele mwankhalwe zaka makumi aŵiri. Nthaŵi imeneyo Debora mneneri wamkazi, mkazi wa Lapidoti, ndiye amene ankatsogolera Aisraele. Iye ankakhala patsinde pa mtengo wa mgwalangwa wa Debora, pakati pa Rama ndi Betele, m'dziko lamapiri la Efuremu, ndipo Aisraele ankabwera kwa iye kuti aŵaweruze. Deborayo adatuma munthu kuti akaitane Baraki, mwana wa Abinowamu, wa ku Kedesi m'dziko la Nafutali. Baraki atabwera, Debora adamuuza kuti, “Chauta, Mulungu wa Aisraele, akukulamula kuti, ‘Pita ukasonkhanitse anthu ako ku phiri la Tabori, ndipo utenge anthu 10,000 m'fuko la Nafutali ndi m'fuko la Zebuloni. Ine ndidzamkopa Sisera, mtsogoleri wa ankhondo a Yabini, kuti adzakumane nanu ku mtsinje wa Kisoni, atatenga magaleta ake ndi ankhondo ake, ndipo ndidzampereka m'manja mwanu.’ ” Baraki adayankha kuti, “Mukapita, nanenso ndipita, koma mukapanda kupita, inenso sindipita.” Debora adati, “Chabwino, ndipita nanu, komatu inu simudzalandirapo ulemu mutapambana, pakuti Chauta adzapereka Sisera m'manja mwa munthu wamkazi.” Tsono Debora adanyamuka kupita ku Kedesi pamodzi ndi Baraki. Baraki adaitana mafuko a Zebuloni ndi a Nafutali kuti abwere ku Kedesi. Anthu amene adamtsata analipo 10,000, ndipo Debora adapita nawo limodzi. Nthaŵi imeneyo Mkeni wina, dzina lake Hebere, anali atadzipatula mwa Akeni anzake, zidzukulu za Hobabu, mlamu wa Mose, ndipo adakamanga hema lake kutali, pafupi ndi mtengo wa thundu ku Zananimu, pafupi ndi Kedesi. Tsono pamene Sisera adamva kuti Baraki, mwana wa Abinowamu, wapita ku phiri la Tabori, adaitanitsa magaleta ake achitsulo 900 onse aja ndi anthu onse amene anali naye. Iwo adanyamuka kuchokera ku Haroseti-Goimu mpaka ku mtsinje wa Kisoni. Debora adauza Baraki kuti, “Dzukani, ndi lero tsiku limene Chauta wapereka Sisera m'manja mwanu. Kodi suja Chauta wakutsogolerani kale?” Pamenepo Baraki adatsika phiri la Tabori, anthu 10,000 akumtsata. Ndipo Chauta adasokoneza Sisera ndi magaleta ake onse, pamodzi ndi ankhondo ake onse. Baraki ndi ankhondo ake ankaŵatsata pambuyo alikupha anthu ambiri. Sisera adatsika pa galeta lake nayambapo kuthaŵa pansi. Baraki adalondola magaletawo ndi ankhondowo mpaka ku Haroseti-Goimu, ndipo ankhondo onse a Sisera adaphedwa ndi lupanga. Palibe munthu ndi mmodzi yemwe amene adapulumuka. Koma Sisera adathaŵa pansi mpaka kukafika ku hema la Yaele, mkazi wa Hebere, Mkeni uja, pakuti panali mtendere pakati pa Yabini, mfumu ya ku Hazori, ndi banja la Hebere Mkeniyo. Yaele adatuluka kukachingamira Sisera, namuuza kuti, “Loŵani mommuno mbuyanga, loŵani. Musaope kanthu.” Choncho adaloŵa m'hemamo ndipo adamfunditsa bulangete. Siserayo adamuuza mkaziyo kuti, “Pepani ndithu mai, patseniko madzi akumwa pang'ono, ndili ndi ludzu.” Mkaziyo adatsekula thumba lachikopa la mkaka nampatsa kuti amwe, namfunditsanso bulangete. Kenaka adauza mkazi uja kuti, “Mukaime pakhomo pa hema, ndipo munthu aliyense akabwera ndi kukufunsani kuti, ‘Kodi muli munthu m'menemo?’ Mumuuze kuti, Ai, mulibe.” Koma Yaele, mkazi wa Hebere, adakatenga chikhomo cha hema, nakatenganso nyundo m'manja mwake, ndipo adayenda monyang'ama napita kwa Sisera uja. Pamene iyeyo anali m'tulo chifukwa chotopa, mkazi uja adakhomera chikhomo chija m'litsipa mwake. Chidatulukira kwinaku mpaka kuloŵa m'nthaka, iye kufa nkukhala komweko. Pamene Baraki adabwera akulondola Sisera, Yaele adatuluka kukamchingamira, namuuza kuti, “Loŵani, ndikuwonetseni munthu amene mukumfunayo.” Iye adaloŵa m'hema la mkaziyo, ndipo adangoona Sisera ali thasa pansi atafa, chikhomo cha hema chili tototo m'litsipa mwake. Motero tsiku limenelo Mulungu adagonjetsa anthu a Yabini, mfumu ya ku Kanani, pamaso pa Aisraele. Ndipo Aisraele adapanikizabe Yabini, mfumu ya ku Kanani, mpaka kumuwonongeratu. Tsiku limenelo la kupambana kwa Debora ndi Baraki, mwana wa Abinowamu, adaimba nyimbo iyi yakuti, “Pakuti atsogoleri adatsogoleradi m'dziko la Israele, ndipo anthu adadzipereka okha mwaufulu, tamandani Chauta. “Imvani, inu mafumu, tcherani khutu, inu olamulira. Ndidzaimba nyimbo yokoma, kuimbira Chauta, Mulungu wa Israele. “Inu Chauta, pamene munkatuluka m'Seiri, pamene munkayenda kuchokera ku Edomu, dziko lidagwedezeka, kumlengalenga kudanjenjemera, mitambo idasungunuka nigwetsa madzi. Mapiri adagwedezeka pamaso pa Chauta, phiri la Sinai lidagwedezeka pamaso pa Chauta, Mulungu wa Aisraele. “Pa nthaŵi ya Samigara, mwana wa Anati, pa nthaŵi ya Yaele, m'miseu munali zii, alendo ankangolambalala m'tinjira takumbali. Anthu adaathaŵa ku midzi, midzi idaatha ku Israele, mpaka pamene iwe Debora udafika, udafika ngati mai ku Israele. Pamene anthu adasankhula milungu ina, nkhondo idafika m'dziko. Mwa anthu 40,000 ku Israele, ndani adatenga chishango kapena mkondo? Mtima wanga uli ndi atsogoleri a ankhondo a ku Israele, uli ndi anthu amene adadzipereka mwaufulu, kudzipereka mwaufulu pakati pa anzao. Tamandani Chauta! “Inu okwera pa abulu oyera ambee, inu okwera pa zishalo, ndi inu oyenda pa mseu, musimbe zimenezi. Ku zitsime oimba akuimba nyimbo zokondwerera kuti Chauta wagonjetsa, zokondwerera kuti anthu ake ku Israele apambana.” “Tsono anthu a Chauta adasonkhana kuchokera ku midzi yao. “Adati, ‘Tsogolera ndiwe Debora, tsogolera, tsogolera ndiwe, tsogolera, imba nyimbo. Pita patsogolo Baraki, tsogolera akapolo ako, iwe mwana wa Abinowamu.’ ” Pambuyo pake anthu okhulupirika adabwera kwa atsogoleri ao, anthu a Chauta adapita kukamenyera Chauta nkhondo, polimbana ndi adani amphamvu. Adakaloŵa m'chigwa kuchokera ku Efuremu, akukutsata iwe Benjamini, pamodzi ndi achibale ako. Kwa Makiri kudachokera atsogoleri a ankhondo, kwa Zebuloni kudachokera onyamula ndodo yaudindo. Olamulira a Isakara adabwera ndi Debora, anthu a kwa Isakara adatsatanso Baraki, nathamangira ku zigwa akumutsata. Anthu a fuko la Rubeni anali osiyana maganizo, osadziŵa chenicheni choyenera kuchita. Chifukwa chiyani ankachedwa ku makola a nkhosa, kumangomvetsera zitoliro zoitanira nkhosa? Anthu a fuko la Rubeni anali osiyana maganizo, osadziŵa chenicheni choyenera kuchita. Agiliyadi adatsala patsidya pa Yordani. Nawonso anthu a kwa Dani, chifukwa chiyani ankachedwa m'zombo? Aasere ankangokhala m'madooko pa gombe la nyanja, ankangokhala m'madooko mwao. Azebuloni ndi fuko limene lidaika moyo wake m'zoopsa. Nawonso Anafutali adaika moyo wao pa minga, pomenya nkhondo pamwamba pa mapiri. “Mafumu adabwera namenya nkhondo, mafumu a ku Kanani adamenya nkhondo ku Taanaki pafupi ndi madzi a ku Megido, koma sadapateko zofunkha zasiliva, kapena china chilichonse. Ngakhale nyenyezi zakumwamba zidamenya nkhondo, zidathira nkhondo Sisera, zikuyenda m'njira zake mu mlengalenga. Chigumula cha madzi a mtsinje wa Kisoni chidaŵakokolola onsewo, madzi othamanga, madzi amphamvu a Kisoni. Mtima wanga, limbika, yenda mwamphamvu! “Tsono ziboda za akavalo zidamveka kwambiri, akavalo ali paliŵiro, akuthamanga kwambiri. “Mngelo wa Chauta akuti, ‘Utemberere Merozi, utemberere koopsa nzika zake, chifukwa chakuti sizidabwere kudzathandiza Chauta, pakulimbana ndi adani ake amphamvu.’ “Yaele, mkazi wa Hebere Mkeni, akhale wodala kupambana akazi onse, ndithudi akhale wodala kupambana akazi onse am'dziko. Munthu uja adapempha madzi akumwa, koma Yaele adamupatsa mkaka, adamupatsa chambiko m'chikho chachifumu. Adatenga chikhomo cha hema natenganso nyundo m'dzanja lake lamanja, adakhoma nacho Sisera, naphwanya mutu wake, adamutswanya ndi kumuboola m'litsipa mwake. Sisera adathifuka naagwa; adangoti thasa ku mapazi a Yaele. Adathifukadi nagwera ku mapazi a Yaele. Kumene adaathifukirako, adagwera komweko, naafa.” Mai wake a Sisera adasuzumira pa zenera, nanena kuti, “Chifukwa chiyani galeta lake silikufika msanga? Bwanji mdidi wa akavalo a magaleta ake ukuchedwa? Amai ake anzeru kopambana adamuyankha, mwiniwake yemwenso adadziyankha yekha kuti, ‘Kodi sakufunafuna zofunkha kuti agaŵane? Akugaŵira wankhondo aliyense mkazi mmodzi kapena aŵiri. Akugaŵira Sisera zofunkha, zovala zonyika mu utoto, zovala zopeta zonyika mu utoto, zovala ziŵiri zonyika mu utoto, zopeta kuti ndizivala m'khosi?’ “Motero Inu Chauta, adani anu aonongeke! Koma abwenzi anu akhale ngati dzuŵa lotuluka ndi mphamvu zake zonse.” Tsono dziko lidakhala pa mtendere zaka makumi anai. Aisraele adachitanso zinthu zoipira Chauta, ndipo Chauta adaŵapereka m'manja mwa Amidiyani zaka zisanu ndi ziŵiri. Amidiyani anali amphamvu ndi oopsa kupambana Aisraele. Nchifukwa chake Aisraele ankakumba malo obisalamo m'mapiri ndiponso m'mapanga, namanganso malinga ao. Aisraele ankati akabzala mbeu, Amidiyani ndi Aamaleke pamodzi ndi anthu akuvuma, ankabwera kudzaŵathira nkhondo. Ankamanga zithando zao moyang'anana ndi Aisraele, ndi kuwononga zokolola zao zonse mpaka ku Gaza, osaŵasiyirako Aisraelewo chakudya chilichonse, nkhosa, ng'ombe kapenanso bulu. Iwo Amidiyani ankabwera ndi ng'ombe zao zomwe pamodzi ndi mahema ao. Ankabwera ambiri ngati dzombe. Kunali kosatheka kuŵaŵerenga anthuwo ndi ngamira zao. Ankaononga dzikolo pamene ankabwera. Motero Amidiyani adalulutsa dziko la Israele kwambiri. Ndipo Aisraele adalira kwa Chauta kuti aŵathandize. Pamene Aisraele adalira kwa Chauta chifukwa cha Amidiyaniwo, Chautayo adaŵatumizira mneneri. Ndipo iye adaŵauza kuti, “Zimene Chauta, Mulungu wa Israele, wanena ndi izi, ‘Ndine amene ndidakutsogolerani kuchokera ku Ejipito, nkukutulutsani m'dziko laukapolo. Ndidakupulumutsani kwa Aejipito ndiponso kwa onse amene ankakuzunzani. Ndidakupirikitsirani adani anu inu mulikufika, ndi kukupatsani dziko lao. Ndidakuuzani kuti Ine ndine Chauta, Mulungu wanu, musapembedze milungu ya Aamori amene mukukhala m'dziko lao, koma inu simudasamale mau anga.’ ” Tsiku lina mngelo wa Chauta adabwera ku Ofura ndi kukhala pansi patsinde pa mtengo wa thundu umene unali wa Yoasi Mwabiyezere. Nthaŵiyo nkuti Gideoni, mwana wake, akupuntha tirigu, atabisala m'nyumba yofinyira mphesa, kuti Amidiyani asamuwone tiriguyo. Apo mngelo wa Chauta uja adamuwonekera namuuza kuti, “Chauta ali nawe, iwe munthu wamphamvu ndi wolimba mtima.” Gideoni adauza mngeloyo kuti, “Pepani mbuyanga, ngati Chauta ali nafe, chifukwa chiyani tsono zonsezi zatigwera? Nanga zili kuti ntchito zake zonse zodabwitsa zimene makolo athu ankatisimbira zakuti ati Chauta adatitulutsa ku dziko la Ejipito? Koma tsopano watitaya, ndipo watipereka kwa Amidiyani.” Chauta adamlamula kuti, “Pita ndi mphamvu zakozi, ukapulumutse Aisraele kwa Amidiyani. Nanga kodi sindine amene ndikukutuma?” Apo Gideoni adayankha kuti, “Inu Chauta, ndapota nanu, kodi ndingathe bwanji kupulumutsa Aisraele? Onani, mbumba yanga ndiye yofooka kwambiri m'fuko la Manase, ndipo m'banja mwa bambo wanga, wamng'ono koposa ndine.” Chauta adamuuza kuti, “Koma Ine ndidzakhala nawe, ndipo udzaŵagonjetsa Amidiyani onse ngati munthu mmodzi.” Tsono Gideoni adati, “Ngati tsopano mwandikomera mtima, onetseni chizindikiro chosonyeza kuti ndinudi Chauta amene mukulankhula nane. Musachoke pano, ndapota nanu, mpaka nditabwerera kwa inu kudzakutulirani chopereka cha chakudya.” Apo Chauta adati, “Chabwino, ndikudikira mpaka utabwerera.” Tsono Gideoni adakaloŵa m'nyumba mwake, nakakonza mwanawambuzi, naphika makeke osatupitsa a ufa wa makilogramu khumi. Nyamayo adaiika m'dengu ndipo msuzi wake adauthira mu mphika, nabwera nazo zonsezo kudzazipereka kwa mngelo uja patsinde pa mtengo wa thundu paja. Mngelo wa Mulunguyo adamuuza kuti, “Tenga nyamayi pamodzi ndi makekeŵa, uziike pathanthwepo, ndi kuthira msuzi pamwamba pake.” Gideoni adachitadi zimenezo. Tsono mngelo wa Chauta adatenga ndodo m'manja mwake nakhudza nayo nyama ija ndi makeke aja. Pompo padabuka moto pathanthwepo ndi kupsereza nyamayo pamodzi ndi makeke aja. Basi mngelo wa Chauta adazimirira osaonekanso. Apo Gideoni adazindikira kuti analidi mngelo wa Chauta, ndipo adati, “Kalanga ine, Chauta Wamphamvuzonse! Ndaona mngelo wa Chauta ndi maso.” Koma Chauta adamuuza kuti, “Mtendere ukhale nawe. Usaope, suufa,” Tsono Gideoni adamangira Chauta guwa pa malo omwewo ndipo adalitcha dzina loti “Chauta ndiye mtendere.” Guwalo lili ku Ofura, mzinda wa Aabiyezere, mpaka lero lino. Usiku umenewo Chauta adauza Gideoni kuti, “Utenge ng'ombe yamphongo ya bambo wako, ng'ombe ina yachiŵiri, ya zaka zisanu ndi ziŵiri, ndipo ugwetse guwa la Baala limene bambo wako ali nalo, ndi kugwetsanso fano la Asera limene lili pambali pake. Kenaka pamwamba pa linga pano umange ndi miyala yoyala bwino guwa la Chauta, Mulungu wako. Tsono utenge ng'ombe yamphongo yachiŵiri ija ndi kuipereka kuti ikhale nsembe yopsereza, pogwiritsa ntchito mtengo wa fano la Asera limene udule ngati nkhunilo.” Choncho Gideoni adatenga anthu khumi mwa atumiki ake, ndipo adachitadi monga momwe Chauta adaamuuzira. Koma popeza kuti ankaopa kwambiri a m'banja la bambo wake ndiponso anthu am'mudzimo, sadachite zimenezo masana, adachita usiku. Pamene anthu am'mudzimo adadzuka m'mamaŵa, adangoona guwa la Baala litagwetsedwa, fano la Asera limene linali pambali pake litadulidwa, ndipo ng'ombe yamphongo yachiŵiri ija itaperekedwa nsembe pa guwa adaamangalo. Ndiye adayamba kufunsana kuti, “Wachita zimenezi ndani?” Atafufuza ndi kufunsafunsa, adati, “Gideoni, mwana wa Yoasi, ndiye amene wachita zimenezi.” Pomwepo anthu am'mudzimo adauza Yoasi kuti, “Mutulutse mwana wako. Ayenera kufa popeza kuti wagwetsa guwa la Baala, ndipo wadula fano la Asera limene linali pambali pake pa guwalo.” Koma onse amene adamuukirawo, Yoasi adaŵauza kuti, “Kodi inu ndinu amene mukuti mummenyere nkhondo Baala? Kodi ndinu amene mukuti mumtchinjirize? Aliyense amene amenyere Baala nkhondo, aphedwa maŵa m'maŵa. Ngati iye ndi mulungudi, adzimenyere nkhondo yekha, popeza kuti guwa lake lagwetsedwa.” Nchifukwa chake pa tsiku limenelo Gideoni adatchedwa Yerubaala, ndiye kuti, “Baala alimbane naye,” poti adaagwetsa guwa lake. Tsono Amidiyani ndi Aamaleke onse, pamodzi ndi anthu onse akuvuma, adasonkhana, ndipo ataoloka Yordani, adakamanga zithando zankhondo m'chigwa cha Yezireele. Koma Mzimu wa Chauta udaloŵa mwa Gideoni. Choncho Gideoniyo adaimba lipenga, ndipo Aabiyezere aja adaitanidwa kuti amtsate. Adatuma amithenga m'dziko lonse la Manase, nawonso Amanasewo adaitanidwa kuti amtsate. Adatumanso amithenga kwa Aasere, Azebuloni ndiponso Anafutali. Onsewo adapita kukaŵachingamira. Gideoni adalankhula ndi Mulungu nati, “Ngati mukuti mupulumutse Aisraele ndi dzanja langa, monga momwe mwaneneramu, chabwino, tsono ine ndikuyala ubweya wankhosa pa malo opunthira tirigu. Mame akangogwa pa ubweya wankhosa pokhapo, koma panthaka nkukhala pouma, apo ndidziŵa kuti Inu mudzapulumutsadi Aisraele kudzera mwa ine, monga momwe mudanenera.” Ndipo zidachitikadi choncho. Pamene adadzuka m'mamaŵa ndi kuufinya ubweya uja, adafinya madzi odzaza mkhate. Tsono Gideoni adalankhulanso ndi Mulungu nati, “Musandipsere mtima, mundilole ndilankhulenso kamodzi kokhaka. Ndapota nanu, mulole kuti paubweya pokhapa pakhale pouma koma panthaka ponsepa pagwe mame.” Mulungu adachitadi momwemo usiku umenewo, mwakuti paubweya pokha panali pouma, koma panthaka ponse padagwa mame. Choncho Yerubaala (ndiye kuti Gideoni) ndi anthu onse amene anali naye, adadzuka m'mamaŵa nakamanga zithando zankhondo pambali pa kasupe wa ku Harodi. Zithando za Amidiyani zinali m'chigwa kumpoto kwao, pafupi ndi phiri la More. Chauta adauza Gideoni kuti, “Anthu uli nawoŵa andichulukira kwambiri, kuti ndigonjetse Amidiyani, chifukwa Aisraele angamandipeputse Ine ndi kumanena kuti, ‘Tadzipulumutsa ndi mphamvu zathu.’ Tsono ulengeze kwa anthu kuti, ‘Aliyense amene akuchita mantha ndi kunjenjemera, abwerere kwao.’ ” Ndiye anthu okwanira 22,000 adabwerera, natsala 10,000. Chauta adauzanso Gideoni kuti, “Anthuŵa akundichulukirabe kwambiri. Uŵatenge, upite nawo ku madzi, ndipo ndikaŵayesa ndine m'malo mwako kumeneko. Amene ndikuuze kuti, ‘Uyu apite nao,’ adzapita nao. Ndipo amene ndikuuze kuti, ‘Uyu asapite nao,’ sadzapita nao.” Choncho Gideoni adapita nawo anthu aja kumadziko. Ndipo Chauta adamuuza kuti, “Onse amene akhathire madzi pakumwa ndi lilime, monga m'mene amachitira galu, uŵaike paokha. Ndipo onse amene agwade kuti amwe madzi, uŵaikenso paokha.” Tsono chiŵerengero cha anthu amene adakhathira madzi pakumwa ndi manja chinali anthu 300. Koma anthu ena onse otsala adagwada pansi kuti amwe madzi. Ndipo Chauta adauza Gideoni kuti, “Ndidzakupulumutsani ndi anthu 300 okhaŵa amene adakhathira pakumwa madzi, ndipo ndidzapereka Amidiyani m'manja mwako. Koma ena onsewo apite kwao.” Choncho Gideoni adatumiza onse kwao kupatula anthu 300 aja. Tsono osankhidwawo adatenga chakudya ndi malipenga a anthuwo. Zithando zankhondo za Amidiyani zinali chakumunsi m'chigwa. Usiku womwewo Chauta adauza Gideoni kuti, “Dzuka, pita ukazithire nkhondo zithandozo, pakuti ndazipereka m'manja mwako. Koma ngati ukuwopa, uyambe wapita kuzithandoko pamodzi ndi Puri mtumiki wako. Udzamva zimene akulankhula, kenaka udzalimba mtima ndipo udzapita kukazithira nkhondo zithandozo.” Pomwepo Gideoni, pamodzi ndi Puri mtumiki wake, adapita ku mbali ina ya zithandozo, kumene kunali ankhondo. Amidiyani ndi Aamaleke ndi anthu akuvuma adaaphimba chigwa chonse ngati dzombe chifukwa cha kuchuluka kwao. Ndipo ngamira zao zinali zosaŵerengeka ngati mchenga wa m'mbali mwa nyanja. Tsono atafika pafupi, Gideoni adamva munthu akufotokozera mnzake maloto ake. Ankati, “Ine ndalota maloto. Ndinangoona mtanda wa buledi wabarele ukugubuduzika kutsikira ku zithando za Amidiyani ndipo unafika mpaka ku chithando china nuchigunda, kotero kuti chinagwa ndipo nkuphwasukaphwasuka.” Ndipo mnzake uja adayankha kuti, “Zimenezi si kanthu kena koma nkhondo ya Gideoni, mwana wa Yoasi, munthu wa ku Israele. Mulungu wapereka Midiyani pamodzi ndi ankhondo ake onse m'manja mwake.” Gideoni atamva kufotokoza kwa malotowo pamodzi ndi kumasulira kwake, adagwada pansi nathokoza Mulungu, ndipo adabwerera ku zithando za Aisraele naŵauza kuti, “Dzukani, Chauta wapereka Amidiyani m'manja mwanu.” Adaŵagaŵa anthu 300 aja m'magulu atatu, napereka malipenga ndi mbiya m'manja mwa onsewo, ndipo m'mbiyamo onse adaikamo nsakali zoyaka. Tsono adauza anthuwo kuti, “Muzindiyang'ana ine, ndipo muchite chimodzimodzi. Ndikafika ku malire a zithando, muchite zomwe ndichite ine. Ndikaimba lipenga, ineyo pamodzi ndi onse amene ali ndi ine, inunso muimbe malipenga ku mbali zonse za zithando zonse, ndipo mufuule kuti, ‘Lupanga la Chauta ndi la Gideoni.’ ” Choncho Gideoni, pamodzi ndi anthu 100 amene anali naye aja, adafika ku malire a zithando pakati pa usiku, alonda atangosinthana chatsopano apa. Tsono adaimba malipenga, naswa mbiya zimene zinali m'manja mwao zija. Apo magulu ena aŵiri aja nawonso adaimba malipenga, naswa mbiya zija, onse atatenga nsakali zija m'dzanja lakumanzere, ndi malipenga oti aziimba m'dzanja lamanja. Ndipo adafuula kuti, “Lupanga la Chauta ndi la Gideoni.” Aliyense adaima pamalo pake mozungulira zithandozo, ndipo ankhondo a m'zithando zija adayamba kuthaŵa akufuula. Ankhondo 300 aja a Gideoni ataimba malipenga, Chauta adamenyanitsa ankhondo aja a Midiyani. Onse adasokonezeka, mwakuti ankamenyana okhaokha. Ankhondowo adathaŵira ku Betesita cha ku Zerera, mpaka ku malire a Abele-Mehola pafupi ndi Tabati. Aisraele a fuko la Nafutali, a fuko la Asere ndi a fuko la Manase lonse, adaitanizana ndipo adapirikitsa Amidiyaniwo. Gideoni adatuma amithenga m'dziko lonse lamapiri la Efuremu kuti akanene kuti, “Tsikani mudzalimbane ndi Amidiyani, ndipo mulande madooko ao oolokera mpaka Betebara ndiponso mtsinje wa Yordani.” Choncho Aefuremu onse adasonkhana, nalanda madooko mpaka ku Betebara ndiponso mtsinje wa Yordani. Adagwira mafumu aŵiri a Midiyani, Orebu ndi Zebu. Adapha Orebu ku thanthwe la Orebu, ndipo Zebu adamuphera ku malo ofinyira mphesa ku Zebu, pamene ankapirikitsa Amidiyani. Tsono adabwera ndi mutu wa Orebu ndi wa Zebu kwa Gideoni kutsidya kwa Yordani. Tsiku lina Aefuremu adamufunsa Gideoni kuti, “Kodi udalekeranji kutiitana ife pamene unkakamenyana ndi Amidiyani?” Ndipo adamkalipira kwambiri. Iye adaŵayankha kuti, “Ndachita chiyani ine kuyerekeza ndi zimene mwachita inu? Kodi zimene mwachita inu Aefuremu si zazikulu koposa zimene fuko langa la Abiyezere lachita? Mulungu wapereka m'manja mwanu mafumu a Midiyani, Orebu ndi Zebu. Ndachita chiyani kuyerekeza ndi zimene mwachita inu?” Gideoni atanena mau amenewo, anthuwo mitima yao idatsika. Gideoni adafika ku Yordani naoloka mtsinjewo, iye pamodzi ndi anthu 300 aja amene nali nawo, atatopa kwambiri, koma akupirikitsabe adani ao. Tsono atafika ku mudzi wa Sukoti, Gideoni adapempha eni mudziwo kuti, “Chonde, apatseniko buledi anthu ali ndi ineŵa, pakuti atopa kwambiri. Tikupirikitsa Zeba ndi Zalimuna, mafumu a Midiyani.” Koma atsogoleri a ku Sukoti adayankha kuti, “Kodi Zeba ndi Zalimuna waŵagonjetsa kale, m'mene ukuti tiŵapatse buledi ankhondo akoŵa?” Gideoni adayankha kuti, “Ai, chabwino! Chauta akapereka Zeba ndi Zalimuna m'manja mwanga, ndidzakukwapulani ndi matsatsa a minga yam'chipululu.” Kuchokera kumeneko adapita ku Penuwele kukapemphanso buledi. Koma anthu a ku Penuwele adamuyankha monga momwe adamuyankhira anthu a ku Sukoti. Apo Gideoni adauza anthu a ku Penuwele kuti, “Pamene ndizikabwerera nditagonjetsa, ndidzagwetsa nsanja ili apayi.” Nthaŵiyo nkuti Zeba ndi Zalimuna ali ku Karikori pamodzi ndi ankhondo ao, anthu pafupi 15,000. Iwoŵa ndiwo amene adatsalako mwa ankhondo a anthu akuvuma, pakuti ankhondo adaafapo 120,000. Gideoni adadzera njira ya anthu okhala m'mahema kuvuma kwa Noba ndi Yogobeha, ndipo adaŵathira nkhondo ankhondowo, pakuti anali osakonzekera. Zeba ndi Zalimuna adathaŵa. Gideoni adaŵapirikitsa nagwira mafumu aŵiri a Midiyaniwo, ndipo ankhondo ao onse adathaŵa ndi mantha. Tsono Gideoni mwana wa Yoasi adabwerako ku nkhondo kudzera ku chikweza cha Heresi. Kumeneko adagwira mnyamata wa ku Sukoti, nayamba kumfunsa mafunso. Mnyamatayo adalembera Gideoni maina a atsogoleri ndi a akuluakulu ena a ku Sukoti, okwanira makumi asanu ndi aŵiri. Apo Gideoni adabwera kwa anthu a ku Sukoti naŵauza kuti, “Naŵa anthu aja, Zeba ndi Zalimuna, aja munkandinena nawoŵa kuti, ‘Kodi Zeba ndi Zalimuna waŵagonjetsa kale, m'mene ukuti tiŵapatse buledi anthu ako otopa kwambiriŵa?’ ” Pamenepo Gideoni adagwira akuluakulu amumzindamo, ndipo adatenga matsatsa a minga yam'chipululu, naŵakwapula anthu a ku Sukotiwo. Ndipo adagwetsa nsanja ya ku Penuwele ija, napha anthu onse amumzindawo. Tsono Gideoni adafunsa Zeba ndi Zalimuna kuti, “Kodi anthu amene mudaŵapha ku Tabori aja ankaoneka bwanji?” Iwo adayankha kuti, “Aliyense ankaoneka monga momwe ukuwonekera iwemu. Ankaoneka ngati ana a mfumu.” Gideoni adaŵauza kuti, “Amene aja anali abale anga, ana a mai wanga. Ndikulumbira pamaso pa Chauta kuti, ‘Mukadapanda kuŵapha, inenso sindikadakuphani.’ ” Apo adauza Yetere, mwana wake wachisamba, kuti, “Tiye, ipha anthuŵa.” Koma mnyamatayo sadasolole lupanga lake pakuti ankaopa, chifukwa anali akali mnyamata. Tsono Zeba ndi Zalimuna adauza Gideoni kuti, “Mutiphe ndinu, pakuti inuyo ndiye muli ndi mphamvu za munthu wamkulu.” Pamenepo Gideoni adapha Zeba ndi Zalimuna. Ndipo adachotsa mphande zimene zinali m'khosi mwa ngamira zao. Tsono Aisraele adamuuza Gideoni kuti, “Muzitilamulira inuyo, mwana wanu ndi zidzukulu zanu, pakuti ndinu amene mwatipulumutsa kwa Amidiyani.” Koma Gideoni adaŵayankha kuti, “Ine sindidzakulamulirani, mwana wanganso sadzakulamulirani. Chauta ndiye amene adzakulamulirani.” Gideoni adaŵauzanso kuti, “Ndikupempheni kanthu kamodzi. Aliyense mwa inu andipatse ndolo zimene adafunkha.” (Adani aja anali ndi ndolo zagolide chifukwa chakuti anali Aismaele). Iwo adayankha kuti, “Tikuvomera kukupatsani zimenezi.” Apo adayala chovala, ndipo munthu aliyense adaponyapo ndolo zofunkhazo. Kulemera kwake kwa ndolo zagolide zimene anthu adaperekazo kunali makilogramu 20, osaŵerengera kulemera kwa mphande, ukufu wam'khosi, zovala zofiira za mafumu a Midiyani, ndiponso malamba am'khosi a ngamira. Ndi golideyo adapanga efodi naikhazika mu mzinda wake ku Ofura. Tsono Aisraele onse adasiya Mulungu nayamba kupembedza efodiyo kumeneko, ndipo idasanduka msampha kwa Gideoniyo ndi kwa banja lake. Choncho Amidiyani adagonjetsedwa ndi Aisraele ndipo sadayesenso zoŵaukira. Motero dziko lidakhala pa mtendere zaka makumi anai pa nthaŵi ya Gideoni. Gideoni mwana wa Yoasi adapita kukakhala kwao. Tsono anali nawo ana 70, akeake ndithu, pakuti anali ndi akazi ambiri. Mzikazi wake wina amene anali ku Sekemu, adamubaliranso mwana dzina lake Abimeleki. Gideoni, mwana wa Yoasi, adafa ndi ukalamba, naikidwa m'manda a Yoasi bambo wake ku Ofura, mzinda wa Abiyezere. Atangomwalira Gideoni, Aisraele adayambanso kupembedza Abaala, nasandutsa Baala wa Chipangano mulungu wao. Aisraelewo sadakumbukirenso Chauta, Mulungu wao, amene adaŵapulumutsa kwa adani ao onse a mbali ndi mbali. Ndipo sadaonetse mtima wothokoza kwa banja la Yerubaala (ndiye kuti Gideoni), chifukwa cha zabwino zonse zimene iye adaŵachitira. Tsono Abimeleki, mwana wa Yerubaala, adapita ku Sekemu kwa achibale a mai wake, nakaŵauza iwowo ndi fuko la banja la mai wake kuti, “Funsani nzika zonse za ku Sekemu kuno kuti, ‘Chabwino koposa nchiti kwa inu, kuti ana onse 70 a Yerubaala azikulamulirani, kapena kuti mmodzi yekha azikulamulirani? Muzikumbukiratu kuti paja ine ndine mbale wanu weniweni.’ ” Achibale a mai wakewo adamlankhulirako kwa anthu onse a ku Sekemu ndipo mitima yao ya anthuwo inali pa Abimeleki pakuti ankati, “Ameneyu ndi mbale wathu.” Adampatsa ndalama zasiliva 70 za m'nyumba yachipembedzo ya Baala wa Chipangano. Ndalama zimenezo Abimeleki uja adaalembera anthu aganyu achabechabe ndi osasamala ntchito kuti azimtsata. Adapita ku nyumba ya bambo wake ku Ufura, nakaŵaphera pa mwala umodzi abale ake 70, ana a Yerubaala. Koma Yotamu, mzime wa Yerubaala, sadaphedwe nao chifukwa adaabisala. Tsono nzika zonse za ku Sekemu zidasonkhana ndi anthu a ku nyumba ya Betemilo, nkupita ku mtengo wa thundu pafupi ndi chipilala chachipembedzo cha ku Sekemu, kukalonga Abimeleki ufumu. Yotamu atamva zimenezi, adapita kukaima pamwamba pa phiri la Gerizimu, ndipo adafuula kwambiri kuti, “Tamverani inu anthu a ku Sekemu, kuti nanunso Mulungu akumvereni. Padangotere: mitengo idapita kukalonga mfumu yoti iziilamulira. Ndiye mitengoyo idauza mtengo wa olivi kuti, ‘Iwe ukhale mfumu yathu.’ Koma mtengo wa oliviwo udalandula, udati, ‘Ine sindingasiye mafuta angaŵa amene amalemekezera milungu ndi anthu omwe, kuti ndizikalamulira mitengo.’ Apo mitengoyo idauza mkuyu kuti, ‘Bwera ndiwe, ukhale mfumu yathu.’ Koma mkuyuwo udalandula, udati, ‘Ine sindingasiye zipatso zanga zokomazi nkuzuna kwakeku, kuti ndizikalamulira mitengo.’ Tsono mitengo ija idauza mtengo wamphesa kuti, ‘Bwera ndiwe, ukhale mfumu yathu.’ Koma mtengo wamphesawo udalandula, udati, ‘Ine sindingasiye kupereka vinyo amene amasangalatsa milungu ndi anthu omwe, kuti ndizikalamulira mitengo.’ Apo mitengo yonse ija idauza mkandankhuku kuti, ‘Bwera ndiwe ukhale mfumu yathu.’ Mkandankhukuwo udayankha kuti, ‘Ngati mukundidzoza ndi mtima wonse kuti ndikhale mfumu yanu, bwerani mudzabisale mumthunzi mwangamu. Mukapanda kutero, moto utuluke mwa ine ndi kupsereza mikungudza ya ku Lebanoni.’ ” Yotamu popitiriza adati, “Kodi tsono mudachita ndi mtima wonse ndiponso mokhulupirika pakumdzoza Abimeleki kuti akhale mfumu? Kodi mwamchitira ulemu Yerubaala ndi banja lake, poyang'anira ntchito zimene adachita? Suja bambo wanga adakumenyerani nkhondo naika moyo wake m'zoopsa, kuti akupulumutseni kwa Amidiyani? Koma lero inu mwaukira banja la bambo wanga. Mwapha ana ake 70 pa mwala umodzi, ndipo mwalonga ufumu Abimeleki, mwana wa mzikazi wake, kuti azilamulira nzika za ku Sekemu, chifukwa chakuti ngwapachibale wanu. Tsono ngati zimene lero mwachitira Yerubaala ndi banja lake mwazichita ndi mtima wonse ndiponso mokhulupirika, mukondwere naye Abimelekiyo ndipo nayenso akondwere nanu. Koma ngati sizili choncho, moto utuluke mwa Abimeleki, upsereze nzika za ku Sekemu pamodzi ndi anthu a ku nyumba ya Betemilo. Ndipo moto utuluke mwa nzika za ku Sekemu ndiponso mwa anthu a ku nyumba ya Betemilo ndi kupsereza Abimeleki.” Tsono Yotamu adathaŵa napita ku Beere ndipo adakakhala komweko, kuwopa Abimeleki mbale wake. Abimeleki adalamulira Aisraele zaka zitatu. Mulungu adaika chidani pakati pa Abimeleki ndi anthu a ku Sekemu, ndipo anthu a ku Sekemuwo adamuukira Abimeleki. Izi zidachitika kuti zoipa zimene iye adaŵachita ana 70 a Yerubaala aja zimubwerere, ndipo kuti magazi ao akhale pa Abimeleki mbale wao amene adaŵaphayo, ndiponso pa anthu a ku Sekemu amene adamulimbitsa mtima kuti aphe abale ake. Motero anthu a ku Sekemu adaika anthu pamwamba pa mapiri kuti abisalire Abimeleki, ndipo ankaŵalanda zinthu zao anthu onse odzera njira imeneyo. Abimeleki zimenezi adazimva. Tsiku lina Gaala, mwana wa Ebedi, adasamukira ku Sekemu pamodzi ndi achibale ake. Ndipo anthu a ku Sekemu adamkhulupirira iyeyo. Anthuwo adapita ku munda kukathyola mphesa, nafinya mphesazo. Kenaka adachita chikondwerero nakaloŵa m'nyumba ya milungu yao. M'menemo adadya ndi kumwa ndipo adayamba kutukwana Abimeleki. Pambuyo pake Gaala, mwana wa Ebedi, adati, “Kodi ife ndife anthu otani m'Sekemu muno? Chifukwa chiyani tikutumikira Abimeleki? Ndipo kodi ndaninso amene uja? Ha, si mwana wa Gideoni! Zebuli amalamulidwa ndi iye uja, koma nanga ife kuti tizimtumikira nchifukwa chiyani? Tiyeni tikhale pambuyo pa kholo lathu Hamori, tate wa fuko lathu. Anthu amumzindamu akadakhala pansi pa ulamuliro wanga, bwenzi nditamchotsa Abimelekiyo, ndipo ndikadamuuza kuti, ‘Onjezera ankhondo ako ndipo bwera, timenyane nkhondo.’ ” Pamene Zebuli, munthu wolamulira mzindawo, adamva mau a Gaala mwana wa Ebedi, adapsa mtima. Adatuma amithenga kwa Abimeleki ku Aruma kukanena kuti, “Gaala, mwana wa Ebedi, pamodzi ndi achibale ake, abwera ku Sekemu, akuutsa mitima ya anthu mu mzinda kuti akuukireni. Nchifukwa chake, mupite usiku inuyo ndi anthu amene muli nawo, kukabisala m'minda. Tsono m'maŵa dzuŵa likamatuluka, mudzuke msanga, mukauthire nkhondo mzindawo. Pamene Gaalayo ndi anthu ake azibwera kudzalimbana nanu, muŵakanthe monga m'mene mungathere.” Choncho Abimeleki ndi anthu onse amene anali naye adadzuka usiku nakabisalira mzinda wa Sekemu m'magulu anai. Gaala mwana wa Ebedi adatuluka nakaima pa khomo la chipata cha mzinda. Ndipo Abimeleki ndi anthu ake adavumbuluka kumene adabisala kuja. Gaala ataŵaona anthuwo, adauza Zebuli kuti, “Ona, anthu akutsika kuchokera pamwamba pa mapiri.” Zebuli adayankha kuti, “Si anthu amenewo, ndi zithunzithunzi chabe zapamapiri zonga anthu.” Gaala adalankhulanso nati, “Ona, anthu akutsika kuchokera pakati penipeni pa phiri, ndipo gulu limodzi likuchokera mbali ya ku mtengo wa thundu wa amaula.” Tsono Zebuli adamufunsa kuti, “Pakamwa pako paja pali kuti tsopano, iweyo amene unkati, ‘Abimeleki ndaninso kuti ife tizimtumikira?’ Kodi si ameneŵa anthu aja unkaŵanyozaŵa? Tulukatu tsopano ukamenyane nawo nkhondo.” Gaala adatuluka akutsogolera anthu a ku Sekemu nakamenyana naye nkhondo Abimeleki. Koma Abimelekiyo adampirikitsa ndipo Gaalayo adathaŵa. Anthu ake ambiri adavulala njira yonse mpaka ku khomo la chipata. Abimeleki adakhazikika ku Aruma, ndipo Zebuli adapirikitsa Gaala pamodzi ndi achibale ake, kotero kuti sadathenso kukhala ku Sekemu. M'maŵa mwake anthu a ku Sekemu adapangana kuti apite ku minda, ndipo Abimeleki adazimva zimenezi. Iye adatenga anthu ake, adaŵagaŵa m'magulu atatu, nakabisala m'minda. Ataona anthu akutuluka mu mzinda, pompo adapita kukalimbana nawo, naŵapha onsewo. Abimeleki pamodzi ndi gulu lake adathamangira kutsogolo, nakakhalira pa khomo la chipata cha mzinda, ndipo nthaŵi yomweyo magulu aŵiri ena aja adaŵathamangira anthu onse amene anali m'minda aja, naŵapha. Nkhondo idakhala tsiku lathunthu. Abimeleki adalanda mzindawo, naŵapha anthu amene anali m'menemo. Adauwonongeratu mzinda wonsewo, nauwaza mchere. Anthu onse a ku nsanja ya Sekemu atamva zimenezo, adakaloŵa m'linga la nyumba yachipembedzo ya Baala wa Chipangano. Abimeleki adazimva zakuti anthuwo asonkhana kumeneko. Tsono adapita ku phiri la Zalimuna ndi anthu ake onse. Kumeneko adatenga nkhwangwa m'manja mwake nadula nthambi za mtengo, ndipo adazinyamula nazisenza pa phewa. Tsono adauza anthu akewo kuti, “Zimene mwaona ndikuchitazi, fulumirani inunso muchite chimodzimodzi, monga momwe ndachitira inemu.” Choncho aliyense adadula mtolo wake natsatira Abimeleki, nakayedzeka mtolo wakewo pa linga lija ndipo adaliyatsa moto, kotero kuti anthu onse a ku nsanja ya Sekemu adafa. Analipo anthu ngati chikwi chimodzi, amuna ndi akazi. Pambuyo pake, Abimeleki adapita ku Tebezi. Adauzinga mzindawo naulanda. Mumzindawo munali nsanja yolimba, ndipo anthu onse amumzindamo, amuna onse ndi akazi omwe, adathaŵira m'nsanjamo, nadzitsekera m'kati. Ndipo adakwera ku tsindwi la nsanjayo. Abimeleki adabwera ku nsanja ija, naithira nkhondo, ndipo adakafika pafupi ndi chitseko cha nsanjayo kuti achitenthe. Koma mkazi wina wake adaponya mwala wa mphero pa mutu wa Abimeleki, nautswanya. Apo Abimeleki uja adaitana msangamsanga mnyamata wake womunyamulira zida zake zankhondo namuuza kuti, “Solola lupanga lako, unditsirize, sindifuna kuti anthu azikati, ‘Mkazi ndiye amene adamupha.’ ” Apo mnyamata wakeyo adambayadi ndi lupanga, mpaka kutulukira kunja lupangalo, naafa. Aisraele ataona kuti Abimeleki wafa, onse adapita kwao. Umu ndimo m'mene Mulungu adalipsirira tchimo la Abimeleki limene adachitira bambo wake, pakupha abale ake 70 aja. Mulungu adaŵalanganso anthu a ku Sekemu chifukwa cha kuipa kwao, ndipo matemberero aja a Yotamu, mwana wa Yerubaala, adaŵagweradi. Atafa Abimeleki, padabwera winanso wodzapulumutsa Aisraele. Iyeyu anali Tola, mwana wa Puwa, mdzukulu wa Dodo, wa fuko la Isakara. Ankakhala ku Samiri, m'dziko lamapiri la Efuremu. Adaweruza Aisraele zaka 23. Pambuyo pake adamwalira, naikidwa ku Samiri. Atafa Tola padabwera Yairo Mgiliyadi amene adaweruza Aisraele zaka 22. Iyeyu anali nawo ana makumi atatu amene ankakwera pa abulu makumi atatu. Anawo anali nayonso mizinda makumi atatu imene mpaka pano ikutchedwa Havoti-Yairo m'dziko la Giliyadi. Pambuyo pake Yairo adamwalira, naikidwa ku Kamoni. Aisraele adachitanso zoipira Chauta potumikira Abaala ndi Aasitaroti, milungu ya ku Siriya, milungu ya ku Sidoni, milungu ya ku Mowabu, milungu ya Aamoni ndiponso milungu ya Afilisti. Aisraelewo adasiyadi Chauta osamamtumikiranso ai. Tsono Chauta adaŵapsera mtima Aisraele, ndipo adalola kuti Afilisti ndi Aamoni aŵagonjetse. Chaka chimenecho anthuwo adagonjetseratu Aisraele nayamba kuŵasautsa. Pa zaka 18, adakhala akuŵasautsa Aisraele onse amene anali patsidya pa mtsinje wa Yordani m'dziko la Aamori, ku Giliyadi. Ndipo Aamoni adaoloka mtsinje wa Yordani kukamenyana nkhondo ndi fuko la Yuda, la Benjamini ndiponso la Efuremu, kotero kuti Aisraele adazunzika kwambiri. Tsono Aisraele adalira kwa Chauta nati, “Takuchimwirani popeza kuti tasiya Inu Mulungu wathu ndipo tatumikira Abaala.” Chauta adafunsa Aisraele kuti, “Kodi suja Ine ndidakupulumutsani kwa Aejipito, Aamori, Aamoni ndi Afilisti? Pamene Asidoni, Aamaleke ndi Amaoni, adaakusautsani, inu nkundilirira kuti ndikuthandizeni, suja Ine ndidakupulumutsani kwa anthu amene aja? Komabe Ine mwandisiya, mukutumikira milungu ina. Nchifukwa chake sindidzakupulumutsaninso. Pitani mukalirire milungu imene mwaisankhulayo. Ikupulumutseni milungu imeneyo pa nthaŵi ya kuzunzika kwanu.” Apo Aisraele adayankha Chauta kuti, “Ai, tachimwadi ife, tichiteni zimene zikukomereni. Tapota nanu, mungotipulumutsako lero lokha.” Choncho adachotsa milungu yachilendo pakati pao nayamba kutumikira Chauta, ndipo Chauta adamva chisoni poona Aisraele akuzunzika. Nthaŵi imeneyo Aamoni adasonkhana kuti adzamenye nkhondo, ndipo adakamanga zithando zankhondo ku Giliyadi. Aisraele nawonso adasonkhana nakamanga zithando zao ku Mizipa. Tsono anthuwo ndi atsogoleri a Agiliyadi adayamba kufunsana kuti, “Kodi munthu woti ayambe kumenyana ndi Aamoniŵa ndani? Iyeyo ndiye amene akhale mtsogoleri wolamulira anthu onse a ku Giliyadi.” Yefita wa ku Giliyadi anali wankhondo wamphamvu. Bambo wake anali Giliyadi, mai wake anali mkazi wadama. Giliyadi analinso ndi mkazi amene anali ndi ana. Tsono ana amenewo atakula, adampirikitsa Yefita namuuza kuti, “Sudzalandirako choloŵa m'nyumba ya bambo wathu, pakuti ndiwe mwana wa kwa mkazi wina.” Choncho Yefita adaŵathaŵa abale akewo nakakhala m'dziko la Tobu. Kumeneko adakakopa anzake achabechabe kuti azimtsata ndi kunka nasakaza zinthu pamodzi naye. Patapita nthaŵi, Aamoni adadzamenyana nkhondo ndi Aisraelewo. Ndipo pamene Aamoniwo adadzathira nkhondo Aisraele, akuluakulu a ku Giliyadi adapita kukamtenga Yefita ku dziko la Tobu. Akuluakuluwo adauza Yefita kuti, “Bwera udzakhale mtsogoleri wathu kuti timenyane nawo nkhondo Aamoni.” Koma Yefita adaŵafunsa akuluakulu a ku Giliyadiwo kuti, “Kodi suja inu mudadana nane nkundipirikitsa ku nyumba ya bambo wanga? Chifukwa chiyani tsopano mwabwera kwa ine poona kuti muli m'mavuto?” Apo akuluakuluwo adamuyankha Yefita kuti, “Nchimene tabwerera kwa iwe tsopano lino, kuti upite nafe kukamenyana ndi Aamoni, ndipo ukhale mtsogoleri wathu wolamulira anthu onse a ku Giliyadi.” Yefita adaŵauza akuluakulu a ku Giliyadiwo kuti, “Mukandibwezeranso kwathu kuti ndikamenye nkhondo ndi Aamoni, ndipo Chauta akandithandiza kuŵagonjetsa, ndidzakhaladi wokulamulirani.” Akuluakulu a ku Giliyadi aja adamuuza Yefita kuti, “Chabwino, tikuvomera zimene ukunenazi, Chauta ndiye mboni yathu.” Choncho Yefita adapita nawo akuluakulu a ku Giliyadiwo, ndipo anthu akumeneko adamsandutsa mfumu ndi mtsogoleri wao woŵalamulira. Tsono Yefita adabwerezanso kulankhula mau ake omwe aja pamaso pa Chauta ku Mizipa. Pambuyo pake Yefita adatuma amithenga kwa mfumu ya Aamoni kukanena kuti, “Kodi ine ndakulakwirani chiyani kuti muzimenyana nkhondo ndi dziko langa?” Mfumu ya Aamoniyo idaŵayankha amithenga a Yefita kuti, “Chifukwa chakuti Aisraele, pochoka ku Ejipito, adalanda dziko langa kuyambira ku mtsinje wa Arinoni mpaka ku mtsinje wa Yaboki mpakanso ku mtsinje wa Yordani. Tsono mundibwezere dziko mwamtendere.” Yefita adatumanso amithenga kwa mfumu ya Aamoni, kukanena kuti, “Yefita akuti: Aisraele sadalande dziko la Amowabu kapenanso dziko la Aamoni ai. Koma pamene Aisraele ankachoka ku Ejipito, adadzera njira yakuchipululu mpaka ku Nyanja Yofiira nakafika ku Kedesi. Nthaŵi imeneyo Aisraele adatuma amithenga kwa mfumu ya ku Edomu kukaiwuza kuti, ‘Tapota nanu, mutilole kuti tidzere m'dziko mwanu.’ Koma mfumu ya ku Edomuyo sidafune kumva zimenezo. Adatumanso amithenga ena kwa mfumu ya ku Mowabu, koma nayonso sidavomereze zimenezo. Choncho Aisraele adakhala ku Kedesi. Pambuyo pake adanyamuka ulendo wao kudzera ku chipululu nazungulira dziko la Edomu ndi dziko la Mowabu, ndipo adafika kuvuma kwa Arinoni. Koma sadaloŵe m'dziko la Mowabu, pakuti mtsinje wa Arinoni unali malire a dziko la Mowabu. Pambuyo pake Aisraele adatuma amithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankalamula ku Hesiboni. Aisraelewo adamupempha kuti, ‘Tapota nanu, mutilole kuti tidzere m'dziko mwanu popita kwathu.’ Koma Sihoni sadaŵalole Aisraele kuti adzere m'dziko mwake. Kenaka Sihoni adasonkhanitsa anthu ake onse, nakamanga zithando zankhondo ku Yahazi, ndipo adamenyana nkhondo ndi Aisraele. Koma Chauta, Mulungu wa Aisraele, adampereka Sihoniyo pamodzi ndi anthu ake onse m'manja mwa Aisraele naŵagonjetsa. Choncho Aisraele adalanda chigawo chonse cha dziko la Aamori amene ankakhala m'dzikolo. Adalanda chigawo chonse cha dziko la Aamori kuyambira ku mtsinje wa Arinoni mpaka ku mtsinje wa Yaboki, ndipo kuyambira ku chipululu mpaka ku mtsinje wa Yordani. Choncho ndi Chauta, Mulungu wa Aisraele, amene adalandira Aisraele anthu ake maiko a Aamori. Nanga inu mukufuna kutilandanso maikowo? Khalani ndi dziko limene mulungu wanu Kemosi wakupatsani kuti likhale lanu. Koma maiko onse amene Chauta Mulungu wathu watilandira, akhala athu ndithu. Ndiponso kodi inuyo mukupambana Balaki, mwana wa Zipori, mfumu ya ku Mowabu? Kodi iye uja adaaputanapo ndi Aisraele kapena kumenyana nawo nkhondo? Pa zaka mazana atatu Aisraele ankakhala ku Hesiboni ndi m'milaga yake, ku Aroere ndi m'milaga yake, ndiponso m'mizinda yonse imene ili m'mbali mwa mtsinje wa Arinoni, nanga chifukwa chiyani simunkalanda malowo nthaŵi imeneyo? Choncho ine sindidakuchimwireni, ndipo mukundilakwira pomenyana nane nkhondo. Woweruza ndi Chauta, ndiye amene agamule lero lino pakati pa Aisraele ndi Aamoni.” Koma mfumu ya Aamoni sidasamaleko mau amene Yefita adaitumizira. Tsono Mzimu wa Chauta udatsikira Yefita, ndipo iye adanyamuka nadzera ku Giliyadi ndi ku Manase. Adakafika ku Mizipa, mzinda wa Giliyadi, ndipo kuchokera ku Mizipako adakafika kumbuyo kwa Aamoni. Yefita adalumbira kwa Chauta kuti, “Mukandithandiza kugonjetsa Aamoniŵa, aliyense amene atuluke pakhomo pa nyumba yanga kudzandichingamira pobwerera, nditagonjetsa Aamoniwo, adzakhala wake wa Chauta ndipo ndidzampereka kuti akhale nsembe yopsereza.” Choncho Yefita adaoloka kunka kwa Aamoni kukamenyana nawo nkhondo. Ndipo Chauta adamthandiza kuŵagonjetsa. Adaŵakanthadi kuyambira ku Aroere mpaka pafupi ndi mzinda wa Miniti, mizinda makumi aŵiri pamodzi, ndiponso mpaka ku Abele-Keranimu. Motero Aamoni adagonjetsedwa ndi Aisraele. Pambuyo pake Yefita adabwerera kwao ku Mizipa. Ndipo adangoona mwana wake wamkazi akutuluka kudzamchingamira, akuimba ng'oma ndi kumavina. Iye anali mwana wake mmodzi yekhayo. Analibenso mwana wina, wamwamuna kapena wamkazi. Yefita atamuwona mwana wake wamkaziyo, adang'amba zovala zake nati, “Kalanga ine, iwe mwana wanga! Wandidula mtima ndipo wandibweretsera mavuto aakulu kopambana, pakuti ndidalonjeza Chauta ndi pakamwa pangapa ndipo sindingathe kubweza malumbiro anga.” Mwanayo adayankha kuti, “Atate, ngati mwalonjeza Chauta ndi pakamwa panu, chiteni zimene mwalonjeza, pakuti tsopano Chauta wakuthandizani kulipsira Aamoni, adani anu.” Iye adamuuzanso bambo wakeyo kuti, “Mundichitire ichi chokha. Bandilekani miyezi iŵiri ndizikayendayenda ku mapiri, kuti ndizikalira pamodzi ndi anzanga kuti ndikufa ndili namwali.” Bambo wakeyo adamuuza kuti, “Pita.” Adamulola kuti apite pa miyezi iŵiri. Choncho mtsikanayo adachoka pamodzi ndi anzake kunka ku mapiri, namakalira kuti akukafa osakwatiwa, opanda mwana. Miyezi iŵiriyo itatha, adabwerera kwa bambo wake ndipo adamchita monga momwe adaalonjezera. Namwaliyo anali asanadziŵe mwamuna. Motero chidasanduka chizoloŵezi m'dziko la Aisraele, kuti ana aakazi a ku Israele ankapita chaka ndi chaka kukalira maliro a mwana wa Yefita Mgiliyadi uja, masiku anai pa chaka. Aefuremu adakonzeka kuti akamenye nkhondo, ndipo adaolokera ku Zafoni nakafunsa Yefita kuti, “Chifukwa chiyani udaaoloka kukamenya nkhondo ndi Aamoni, ife osatiitana kuti tipite nao? Tikutenthera m'nyumba mwakomu.” Yefita adaŵauza kuti, “Ine ndi anthu anga tidaakangana kwambiri ndi Aamoni. Ndidakuitanani, koma inu simudadzandipulumutse kwa iwowo. Ndipo nditaona kuti simunkafuna kundipulumutsa, ndidangochita utotomoyo nkuwoloka Yordani kukalimbana nawo Aamoni. Chauta adatithandiza kuŵagonjetsa. Chifukwa chiyani tsono mwabwera kwa ine lero lino kuti mudzachite nane nkhondo?” Tsono Yefita adasonkhanitsa anthu onse a ku Giliyadi namenyana nkhondo ndi Aefuremu. Ndipo Agiliyadi adagonjetsa Aefuremu chifukwa chakuti Aefuremuwo ankati, “Inu Agiliyadi ndinu othaŵa ku Efuremu, ochokera pakati pa Aefuremu ndi Amanase.” Ndipo Agiliyadi adalanda Aefuremu madooko a mtsinje wa Yordani. Pamene aliyense wothaŵa ku Efuremu ankati, “Ndiloleni ndiwoloke,” Agiliyadi ankamufunsa kuti, “Kodi ndiwe Mwefuremu?” Iye akayankha kuti, “Ai”, iwo ankamuuza kuti, “Chabwino, nena kuti, ‘Shiboleti.’ ” Munthuyo ankati, “Siboleti,” pakuti sankatha kutchula bwino mauwo. Ankamugwira ndi kumupha pompo pa madooko a mtsinje wa Yordani. Nthaŵi imeneyo adaphedwa Aefuremu 42,000. Yefita adaweruza Aisraele zaka zisanu ndi chimodzi. Pambuyo pake Yefita, amene anali Mgiliyadi, adamwalira, ndipo adaikidwa mu mzinda wake wa Giliyadi. Atafa Yefita, Ibizani wa ku Betelehemu adaweruza Aisraele. Iyeyu anali ndi ana aamuna makumi atatu ndiponso ana aakazi makumi atatu. Adakwatitsa ana aakazi makumi atatuwo kwa anthu osakhala a fuko lake, ndipo adakatengera ana ake aamuna aja ana aakazi makumi atatu a fuko lachilendo. Ibizaniyo anali mtsogoleri wa Aisraele zaka zisanu ndi ziŵiri. Pambuyo pake adamwalira, ndipo adaikidwa ku Betelehemu. Ibizani atafa, Eloni Mzebuloni adasanduka mtsogoleri wa Aisraele. Iyeyu adatsogolera Aisraele zaka khumi. Pambuyo pake adamwalira, naikidwa ku Ayaloni m'dziko la Zebuloni. Atafa iyeyo, Abidoni mwana wa Hilele Mpiratoni, adatsogolera Aisraele. Iye anali ndi ana aamuna makumi anai ndi adzukulu makumi atatu amene ankakwera pa abulu makumi asanu ndi aŵiri. Iye adatsogolera Aisraele zaka zisanu ndi zitatu. Ndipo Abidoniyo adamwalira, naikidwa ku Piratoni m'dziko la Efuremu, ku mapiri a Aamaleke. Aisraele adachimwiranso Chauta. Ndipo Chauta adaŵapereka m'manja mwa Afilisti pa zaka makumi anai. Ku Zora kunali munthu wina, wa fuko la Dani, dzina lake Manowa. Mkazi wake analibe ana, anali wosabereka. Mngelo wa Chauta adamuwonekera mkaziyo namuuza kuti, “Inu mai, ngakhale mpaka pano muli opanda ana, komabe mudzakhala ndi pathupi ndipo mudzabala mwana wamwamuna. Ndiye inu mudzisamale bwino, musamamwe vinyo kapena chakumwa china choledzeretsa, ndipo musamadye chakudya chilichonse chosaloledwa. Pakuti ndithu mudzakhala ndi pathupi ndipo mudzabala mwana wamwamuna. Mwanayo akadzabadwa, kumutu kwake kusadzapite lumo, pakuti mnyamatayo adzakhala Mnaziri, ndiye kuti wopatulikira Mulungu kuyambira tsiku la kubadwa kwake. Ndipo adzayambapo ntchito yopulumutsa Aisraele kwa Afilisti.” Tsono mkaziyo adadzauza mwamuna wake kuti, “Munthu wa Mulungu anabwera kuno, ndipo nkhope yake inali yoopsa kwambiri ngati nkhope ya mngelo wa Mulungu. Sindidamufunse kumene akuchokera, iyenso sadandiwuze dzina lake. Koma anandiwuza kuti, ‘Mudzakhala ndi pathupi ndipo mudzabala mwana wamwamuna. Ndiye musamamwe vinyo kapena chakumwa china choledzeretsa, ndipo musamadye chakudya chosaloledwa chilichonse, chifukwa mnyamatayo adzakhala Mnaziri, wopatulikira Mulungu, kuyambira tsiku la kubadwa kwake mpaka tsiku la kufa kwake.’ ” Tsono Manowa adapemphera kwa Chauta kuti, “Inu Chauta, ndapota nanu, mulole kuti munthu amene mudaamtuma uja abwerenso, adzatiphunzitse zimene tiyenera kuchita naye mnyamata amene adzabadweyo.” Mulungu adamvera pemphero la Manowa, ndipo mngelo wa Mulungu uja adabweranso kwa mkaziyo nampeza atakhala pansi m'munda. Koma mwamuna wake Manowa sanali nao. Mkazi uja adathamanga nakauza mwamuna wake kuti, “Munthu uja adaabwera kuno tsiku lijaliyu wandiwonekeranso.” Apo Manowa adanyamuka natsata mkazi wake, ndipo adakafika kumene kunali munthuyo nakamufunsa kuti, “Kodi inu ndinu amene mudaalankhula ndi amaiŵa?” Iye adayankha kuti, “Inde ndinedi.” Manowa adamufunsa kuti, “Tsono zimene mudanenazi zikadzachitikadi, kodi mnyamatayo azidzakhala bwanji, ndipo azidzachita chiyani?” Mngelo wa Chauta uja adauza Manowa kuti, “Zonse zimene ndidaŵauza amaiŵa asamale kuti azichitadi. Asati adye chilichonse chochokera ku mphesa, ndipo asati amwe vinyo kapena chakumwa china choledzeretsa kapenanso kudya chinthu chosaloledwa chilichonse. Asunge zonse zimene ndidaŵalamula.” Manowa adauza mngelo wa Chauta kuti, “Pepani, tayambani mwaima, tikuti tikuwotchereni kamwanakambuzi.” Koma mngelo wa Chauta adauza Manowa kuti, “Ngakhaletu mukundidikiritsa chakudyacho, ine sindidya ai. Koma ngati mukonze nsembe yopsereza, muipereke kwa Chauta.” (Monsemo nkuti Manowa ali wosazindikira kuti mlendoyo ndi mngelo wa Chauta.) Apo Manowa adauza mngeloyo kuti, “Timati mutiwuze dzina lanu kuti tidzakulemekezeni, zikadzachitikadi zimene mwanenazi.” Mngelo wa Chautayo adafunsa Manowa kuti, “Chifukwa chiyani mukufuna kudziŵa dzina langa? Dzina laketu nlodabwitsa.” Pamenepo Manowa adatenga kamwanakambuzi pamodzi ndi chopereka cha chakudya, nakapereka nsembe pa thanthwe kwa Chauta, Iye amene amachita zodabwitsa. Pamene malaŵi a moto ankakwera kumwamba kuchokera paguwapo, mngelo wa Chauta uja adakwera m'malaŵi a motowo, Manowa ndi mkazi wake akuyang'ana. Apo iwo adadzigwetsa pansi, naŵeramitsa mitu pansi. Mngelo wa Chauta uja sadaŵaonekerenso Manowa ndi mkazi wake. Choncho Manowa adazindikira kuti anali mngelo wa Chauta. Tsono adauza mkazi wake kuti, “Ife ndiye tifatu basi, nanga sitaona Mulungu!” Koma mkazi wake adati, “Akadakhala kuti Chauta akufuna kutipha, sakadailandira nsembe yathu yopsereza ndi chopereka chathu cha chakudya chija. Ndiponso sakadatiwonetsa zinthu zonsezi kapenanso kutiwuza tsopano zinthu zonga ngati zimenezi.” Motero mkaziyo adabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Samisoni. Mnyamatayo adakula ndipo Chauta adamdalitsa. Ndipo Mzimu wa Chauta udayamba kumlimbitsa pamene anali ku zithando za anthu a fuko la Dani, pakati pa Zora ndi Esitaoli. Samisoni adapita ku Timna ndipo kumeneko adaonako mtsikana wachifilisti. Atabwerera kwao adakauza bambo ndi mai wake kuti, “Ku Timna ndaonako mtsikana wachifilisti. Mukanditengere ameneyo, ndidzamkwatire.” Koma bambo ndi mai wake adamufunsa kuti, “Kodi palibe mkazi woti ungakwatire pakati pa ana a achibale akoŵa kapena pakati pa anthu a mtundu wathu, kuti uzikatenga mkazi pakati pa Afilisti, anthu osaumbalidwa?” Koma Samisoni adauza bambo wake kuti, “Ine ndiye kanditengereni yemweyo, pakuti ndiye ndamkonda kwambiri.” Bambo ndi mai wake sankadziŵa kuti zimenezo zinali zochokera kwa Chauta, pakuti Chauta ankafunafuna poŵapezera chifukwa Afilistiwo. Nthaŵi imeneyo nkuti Afilisti akulamulira Aisraele. Tsono Samisoni adapita ku Timna pamodzi ndi bambo ndi mai wake. Atafika ku minda yamphesa ya ku Timna, Samisoni adamva mwanawamkango akumdzumira. Pamenepo Mzimu wa Chauta udamtsikira Samisoni ndi kumsandutsa wankhongono. Motero ngakhale analibe chida m'manja, Samisoni adakadzula mkangowo, monga momwe munthu amakadzulira kamwanakambuzi. Koma sadauze bambo kapena mai wake zimene adachitazo. Tsono Samisoni adapita kukalankhula naye mtsikana uja, ndipo adamkonda kwambiri mtsikanayo. Patapita kanthaŵi Samisoni adabwerera kudzamtenga mtsikanayo. Pa njira adapatuka kukaona mkango adaaupha uja. Adangoona njuchi zili mu mkangowo pamodzi ndi uchi wake. Samisoni adafula njuchizo, natenga uchi m'manja ndi kumapita naadya. Atafika kwa bambo ndi mai wake, adaŵapatsako uchiwo, iwo naadya. Koma sadaŵauze kuti uchiwo adaufula mu mkango wakufa. Bambo wakeyo adapita kunyumba kwa mkazi uja, ndipo Samisoni adakonza phwando kumeneko, pakuti ndi m'mene ankachitira anyamata. Pamene anthu adamuwona, adabwera ndi anyamata makumi atatu kuti akhale naye. Samisoni adaŵauza kuti, “Bwanji ndikuphereni mwambi! Mukandiwuza tanthauzo lake, asanapite masiku asanu ndi aŵiri a phwando, ndidzakupatsani zovala zabafuta makumi atatu ndiponso zovala za tsiku lachikondwerero makumi atatu. Koma mukalephera kundiwuza tanthauzo lake, mudzandipatsa ndinu zovala zabafuta makumi atatu, ndiponso zovala za tsiku lachikondwerero makumi atatu.” Iwo adamuyankha kuti, “Tiphere mwambiwo, tiwumve.” Tsono adaŵauza kuti, “M'chodya zinzake mudatuluka chakudya. M'champhamvu mudatuluka chozuna.” Pa masiku atatu, anthuwo sadathe kuumasula mwambiwo. Tsiku lachinai lake iwo adauza mkazi wa Samisoni kuti, “Umunyengerere mwamuna wako, kuti atiwuze tanthauzo lake la mwambi uja, mwinamwina tikutentha iweyo pamodzi ndi nyumba ya bambo wako. Monga inu mwatiitana kuno kuti mutisandutse osauka?” Choncho mkazi wa Samisoni adayamba kulira pamaso pa mwamuna wake namuuza kuti, “Inu mumadana nane, simundikonda konse. Mwaŵaphera mwambi anthu a m'dziko mwangaŵa, koma ine osandiwuzako tanthauzo lake.” Apo Samisoni adamuuza kuti, “Ona, ngakhale bambo wanga ndi mai wanga sindidaŵauze, ndiye ndingauze iweyo?” Mkaziyo ankangomulirira masiku onse asanu ndi aŵiri aphwandowo. Tsono pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri adamuuza, chifukwa chakuti adaamkakamiza kwambiri. Pompo mkaziyo adakauza anthu a m'dziko mwake aja tanthauzo la mwambiwo. Choncho anthu amumzinda aja adauza Samisoni pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri dzuŵa lisanaloŵe, kuti, “Nchiyani chozuna kuposa uchi? Nchiyani champhamvu kuposa mkango?” Samisoni adaŵauza kuti, “Mukadapanda kulima ndi msotiwang'ombe wanga, simukadatha kumasula mwambi wangawu.” Apo Mzimu wa Chauta udamtsikira Samisoni mwamphamvu ndipo Samisoniyo adapita ku Asikeloni nakapha anthu makumi atatu am'mudzimo ndipo adatenga zovala zao za tsiku lachikondwerero, nazipereka kwa amene adamasula mwambi aja. Ndipo adabwerera ku nyumba ya bambo wake ali wokwiya kwambiri. Nthaŵi yomweyo mkazi wa Samisoni uja bambo wake adamkwatitsa kwa mnzake wa Samisoniyo amene adaali mnzake womuperekeza paukwati paja. Patapita kanthaŵi, pa nyengo yodula tirigu, Samisoni adapita kukacheza kwa mkazi wake, atatenga mwanawambuzi. Ndipo adati, “Ndikufuna kukaloŵa m'chipinda cha mkazi wanga.” Koma bambo wake wa mkaziyo adamkaniza kuloŵa. Bamboyo adamuuza kuti, “Ine ndidaatsimikiza kuti mukudana naye kwambiri mkaziyu. Choncho ndidamkwatitsa kwa mnzanu uja. Kodi mng'ono wake si wokongola kupambana iyeyu? Pepani ndithu, ingotengani ameneyu m'malo mwake.” Samisoni adaŵauza kuti, “Ulendo uno aliyense asandinene, ndikaŵachita choipa chachikulu Afilistiŵa.” Motero Samisoni adakagwira nkhandwe mazana atatu nazimangirira michira ziŵiriziŵiri. Kenaka pa mfundo iliyonse ya michirayo adamangirirapo nsakali naziyatsa. Atayatsa nsakalizo, adazitaya nkhandwezo kuti zipite m'minda yatirigu ya Afilisti. Popitapo zidakatentha milu ya tirigu ndi tirigu wosadula yemwe, pamodzi ndi mitengo ya olivi. Tsono Afilisti adayamba kufunsana kuti, “Ndani wachita zimenezi?” Ena adayankha kuti, “Ndi Samisoni, mkamwini wa Mtimuna uja, amene wachita zimenezi, chifukwa chakuti Mtimunayo watenga mkazi wa Samisoni kumkwatitsa kwa mnzake.” Tsono Afilisti adabwera namtentha mkaziyo pamodzi ndi bambo wake yemwe. Atamva zimenezi Samisoni adati, “Ngati zimenezi nzimene mumachita, ndikulumbira kuti sindileka mpaka nditakulipsirani.” Tsono adamenyana nawo koopsa napha anthu ambiri. Kenaka adakaloŵa ku phanga la ku Etamu, nakhala komweko. Pambuyo pake Afilisti adadzamanga zithando zao zankhondo m'dziko la Yuda, ndipo adathira nkhondo pa Lehi. Anthu a ku Yuda adafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mwadzamenyana nafe?” Iwowo adayankha kuti, “Tabwera kudzamanga Samisoni kuti timchite zomwe iye adatichita ife.” Tsono anthu 3,000 a ku Yuda adapita ku phanga la ku Etamu, namufunsa Samisoni kuti, “Kodi sukudziŵa kuti Afilisti ndiwo amene amatilamulira? Nanga izi watichitazi nzotani?” Iye adaŵayankha kuti, “Ndaŵachita zomwe iwowo adandichita ine.” Tsono iwowo adamuuza kuti, “Tabwera kudzakumanga kuti tikakupereke kwa Afilisti.” Samisoni adaŵauza kuti, “Lonjezeni molumbira kuti simundipha ndi inuyo.” Iwo adamuuza kuti, “Iyai. Ife tingokumanga chabe nkukakupereka kwa iwowo. Sitikupha ai.” Choncho adammanga ndi zingwe ziŵiri zatsopano, namtulutsa m'phanga muja. Samisoni atafika ku Lehi, Afilisti adabwera akufuula kudzamchingamira. Pompo Mzimu wa Chauta udamtsikira mwamphamvu, ndipo zingwe zimene adammanga nazo zija zidasanduka ngati thonje logwira moto, zidachita ngati kusungunuka nkuchoka m'manja mwake. Tsono adapeza chibwano cha bulu amene anali atafa chatsopano. Adachitola, naphera nacho anthu chikwi chimodzi. Apo Samisoni adayamba kuimba nyimbo yakuti, “Ndi chibwano cha bulu, milu ndi milu ya anthu! Ndi chibwano cha bulu, ndapha anthu chikwi chimodzi!” Pambuyo pake, adachitaya pansi chibwano chija, ndipo malowo adatchedwa Ramatilehi. Tsono Samisoni adamva ludzu kwambiri ndipo adatana Chauta mopemba nati, “Inu mwapereka chipulumutso chachikulu choterechi kudzera mwa ine mtumiki wanu. Kodi tsopano ndife ndi ludzu ndi kugwidwa ndi anthu osaumbalidwaŵa?” Pamenepo Mulungu adang'amba nthaka ku Lehi, ndipo madzi adatuluka m'dzenjemo. Samisoni atamwa madziwo, mphamvu zake zidabwereramo, ndipo adatsitsimuka. Nchifukwa chake malowo adatchedwa Enihakore. Malowo ali ku Lehi mpaka pano. Samisoni adatsogolera Aisraele pa nthaŵi ya Afilisti zaka makumi aŵiri. Samisoni adapita ku Gaza ndipo kumeneko adaonako mkazi wadama naloŵa m'nyumba yake. Anthu a ku Gaza adauzidwa kuti, “Samisonitu adabwera kuno.” Tsono anthuwo adazinga malowo namubisalira usiku wonse pa chipata cha mzinda. Iwo adakhala chete usiku wonsewo namanena kuti, “Tiyeni tidikire mpaka m'maŵa kutacha, pamenepo timuphe.” Koma Samisoni adagona mpaka pakati pa usiku. Pakati pa usikupo adadzuka, nagwira zitseko zapachipata ndi mafuremu ake onse aŵiri. Adazizula pamodzi ndi mpiringidzo ndi zina zonse. Adazisenza pa phewa, napita nazo pamwamba pa phiri loyang'anana ndi Hebroni. Pambuyo pake Samisoni adayamba kukonda mkazi wina wa ku chigwa cha Soreki, dzina lake Delila. Akalonga a Afilisti adabwera kwa mkaziyo namuuza kuti, “Umnyengerere mwamunayu, uwone pamene pagona mphamvu zake zoopsazi ndiponso m'mene tingathe kumpambanira, kuti timmange ndi kumgonjetsa. Ukatero, aliyense mwa ife adzakupatsa ndalama zasiliva 1,100.” Tsono Delila adauza Samisoni kuti, “Inu, tandiwuzani, kodi mphamvu zanu zoopsazi zagona poti? Kodi munthu atati akumangeni kuti akugonjetseni, nkofunika kuti atani?” Samisoni adamuuza kuti, “Atandimanga ndi nsinga zatsopano zisanu ndi ziŵiri zosauma, ndidzasanduka wofooka ndipo ndidzafanafana ndi munthu wina aliyense.” Tsono akalonga a Afilisti aja adadzampatsa mkaziyo nsinga zisanu ndi ziŵiri zatsopano zosauma, ndipo iye adamangira mwamuna wake. Nthaŵi imeneyo nkuti mkaziyo ataika anthu ombisalirawo m'chipinda cham'kati. Kenaka adafuula kwa mwamuna wake kuti, “Inu amuna anga, Afilisti aja akubwera.” Koma iye adangomwetula nsingazo monga m'mene imamwetukira nkhosi ya chingwe ikamapsa. Choncho chinsinsi cha mphamvu zakezo sichidadziŵikebe. Apo Delila adauza Samisoni kuti, “Ndithu mwandipusitsa ndi kundinamiza. Chonde tandiwuzani m'mene munthu angakumangireni.” Samisoni adauza mkaziyo kuti, “Atandimanga ndi zingwe zatsopano zimene sadazigwiritse ntchito, ndidzasanduka wofooka, ndipo ndidzafanafana ndi munthu wina aliyense.” Choncho Delila adatenga zingwe zatsopano nammanga nazo, nafuula kwa iye kuti, “Inu amuna anga, Afilisti aja akubwera.” Monsemo nkuti anthu amene ankambisalira aja ali m'chipinda cham'kati. Koma, Samisoni adangomwetula zingwezo kumanja kwake ngati thonje. Pamenepo Delila adauzanso Samisoni kuti, “Mpaka tsopano lino mwakhala mukundipusitsa ndi kumandinamiza. Tandiwuzani m'mene munthu angathe kukumangirani.” Samisoni adamuuza kuti, “Ngati njombi zisanu ndi ziŵiri za kumutu kwanga uzilukirira m'cholukira nsalu ndi kuchimanga molimbika ndi chikhomo, ndidzasanduka wofooka ndipo ndidzafanafana ndi anthu ena.” Choncho pamene Samisoni ankagona, Delila adatenga njombi za kumutu kwa Samisoni nazilukirira m'cholukira nsalu. Ndipo adachimanga molimbika ndi chikhomo nafuula kwa Samisoni kuti, “Inu amuna anga, Afilisti aja akubwera.” Koma iye adadzukira kutulo nazula chikhomocho, ndipo njombi zake zidachoka m'cholukira chija. Apo mkaziyo adamufunsa kuti, “Mungathe bwanji kunena kuti mumandikonda pamene mtima wanu suli pa ine? Mwakhala mukundipusitsa katatu konseka, ndipo simudandiwuze pamene pagona mphamvu zanu zoopsazi.” Tsono pamene adampanikiza ndi mau ake tsiku ndi tsiku ndi kumkakamiza, mtima wa Samisoni udatopa mpaka kufuna kufa. Choncho adamuululira mkaziyo maganizo ake onse namuuza kuti, “Pamutu pangapa sipanapite lumo, popeza kuti ndakhala ndili Mnaziri wopatulikira Mulungu, kuyambira ndili m'mimba mwa mai wanga. Atangondimeta tsitsi langali, mphamvu zanga zidzandichokera. Ndidzasanduka wofooka ndipo ndidzafanafana ndi munthu wina aliyense.” Pamene Delila adaona kuti waulula maganizo ake onse, adatuma uthenga kukaŵaitana akalonga a Afilisti aja ndipo adaŵauza kuti, “Bweraninso kamodzi kokha, pakuti wandiwululira maganizo ake onse.” Tsono akalonga a Afilisti adafika kwa mkazi uja atatenga ndalama m'manja mwao. Mkaziyo adamgonetsa tulo Samisoni pamiyendo pake. Ndipo adaitana munthu kuti amete njombi zisanu ndi ziŵiri za kumutu kwa Samisoni. Pamenepo iyeyo adayamba kufooka ndipo mphamvu zake zidamchokera. Kenaka Delila adafuula kuti, “Inu amuna anga, Afilisti aja akubwera.” Samisoni adadzuka akuganiza kuti, “Ndituluka monga momwe ndimachitira nthaŵi zonse, ndipo ndidzimasula.” Koma sadadziŵe kuti Chauta wamsiya. Pompo Afilisti adamgwira namkoloola maso ake, ndipo adapita naye ku Gaza atammanga ndi maunyolo amkuŵa. Kumeneko ankapera pa mphero m'ndende. Pambuyo pake tsitsi la kumutu kwake lomwe adaalimeta, lidayamba kumeranso. Tsiku lina akalonga a Afilisti adasonkhana kudzapereka nsembe yaikulu kwa Dagoni mulungu wao ndi kudzakondwerera, pakuti ankati, “Mulungu wathu watithandiza kugonjetsa Samisoni, mdani wathu.” Pamene anthu adamuwona, adayamba kutamanda mulungu wao. Ankati, “Mulungu wathu watithandiza kugonjetsa mdani wathu, munthu woononga dziko lathu uja amene adapha anthu ambiri.” Pamene mitima yao inkasangalala adati, “Muitaneni Samisoni kuti adzatisangalatse.” Choncho adamtulutsa m'ndende, ndipo iye adayamba kuŵasangalatsa. Kenaka adamuimiritsa pakati pa mizati. Apo Samisoni adauza mnyamata amene adamgwira dzanja kuti, “Undilole ndikhudze mizati imene yachirikiza nyumba yonseyi, kuti ndiitsamire.” M'menemo nkuti nyumbayo ili yodzaza ndi anthu, amuna ndi akazi. Akalonga onse a Afilisti anali momwemo, ndipo padenga pake panali pafupi anthu 3,000, amuna ndi akazi, amene ankaonera Samisoni akuseŵera. Tsono Samisoni adatama Chauta mopemba nati, “Inu Chauta, kumbukireni kamodzi kokhaka, ndapota nanu, ndipo mundilimbitse Inu Mulungu, kuti ndiŵalipsire Afilistiŵa chifukwa cha maso anga aŵiriŵa.” Pomwepo Samisoni adagwira mizati iŵiri yapakati imene inkachirikiza nyumbayo. Adaitsamira ndi mphamvu zake zonse, dzanja lake lamanja lili pa mzati wina, lamanzere lili pa mzati winanso. Ndipo Samisoni adati, “Ndifere kumodzi ndi Afilistiŵa.” Tsono adakankha ndi mphamvu zake zonse, ndipo nyumbayo idaŵagwera akalonga aja pamodzi ndi anthu onse aja amene anali m'menemo. Choncho kuchuluka kwa anthu amene Samisoni adaŵapha pa nthaŵi ya kufa kwake kudaposa kwa anthu amene iye adaŵapha pa nthaŵi imene anali moyo. Tsono abale a Samisoni adabwera pamodzi ndi banja lao lonse kudzamtenga ndipo adakamuika pakati pa Zora ndi Esitaoli, m'manda a Manowa bambo wake. Samisoni adatsogolera Aisraele zaka makumi aŵiri. Ku dziko lamapiri la Efuremu kunali munthu wina dzina lake Mika. Iyeyu adauza mai wake kuti, “Pamene munthu adaakuberani ndalama zasiliva 1,100, inu mudaamutemberera wakubayo, matembererowo ine ndidaŵamva. Ndalamazo ndi izi, zili ndi ine. Ndine ndidaatenga.” Mai wakeyo adamuuza kuti, “Chauta akudalitse mwana wanga.” Tsono iye adabwezera ndalama zonse kwa mai wake, ndipo maiyo pofuna kuchotsa temberero lija, adati, “Ndikuzipatula ndalama zasilivazi kuti zikhale za Chauta. Ndidzazipereka kuti aseme fano ndi kulikuta ndi siliva. Choncho ndikubwezera ndalamazo.” Tsono Mika atabweza ndalamazo kwa mai wake, mai wakeyo adatengapo ndalama zasiliva 200 nazipereka kwa mmisiri wosula siliva. Munthuyo adasema fano nasungunula ndalamazo, nakutira fanolo ndi siliva. Ndipo Mika adaliimika m'nyumba mwake. Mikayo anali ndi kachisi wakewake, ndipo adapanga chovala chaunsembe cha efodi ndiponso mafano am'nyumba otchedwa terafimu, nakhazika mmodzi mwa ana ake kuti akhale wansembe wake. Masiku amenewo ku Israele kunalibe mfumu. Munthu aliyense ankangochita zimene zinkamkomera. Ku Betelehemu m'dziko la Yuda kunali mnyamata wina wa fuko la Yuda amene anali Mlevi. Munthuyo adachoka ku mudzi wa Betelehemu uja ku Yuda, kukafunafuna kwina kokakhala. Akuyenda ulendo wakewo adakafika ku dziko lamapiri la ku Efuremu ku nyumba ya Mika. Mika uja adamufunsa kuti, “Kodi inu kwanu nkuti?” Munthuyo adayankha kuti, “Ine ndine Mlevi wa ku Betelehemu m'dziko la Yuda, ndikufunafuna koti ndikhale nao.” Apo Mika adamuuza kuti, “Khalani ndi ine, mukhale mlangizi wanga ndi wansembe wanga, ine ndizikupatsani ndalama zasiliva khumi pa chaka, ndizikupatsaninso zovala ndi zakudya.” Mleviyo adavomera kukhala naye munthuyo, ndipo adasanduka ngati mmodzi mwa ana ake. Tsono Mika adalonga Mleviyo unsembe, ndipo iyeyo ankakhala m'nyumba mwa Mika. Apo Mika adati, “Tsopano ndikudziŵa kuti Chauta adzandilemeza, popeza kuti Mleviyu ndiye wansembe wanga.” Masiku amenewo kunalibe mfumu ku dziko la Israele. Anthu a fuko la Dani ankafunafuna dziko loti azikhalamo, kuti likhale choloŵa chao, pakuti mpaka nthaŵi imeneyo nkuti iwowo asanalandire choloŵa pakati pa mafuko a Aisraele. Choncho anthu a fuko la Daniwo adatuma anthu asanu olimba mtima, osankhidwa mwa mabanja ao onse. Anthuwo adachokera ku Zora ndi ku Esitaoli, adatumidwa kuti akazonde dziko ndi kuliyendera. Anthu onse adaŵauza kuti, “Pitani mukayendere dzikolo.” Iwowo adakafika ku dziko lamapiri la ku Efuremu ku nyumba ya Mika, nagona komweko. Ali kunyumba kumeneko, adazindikira liwu la mnyamata wachilevi uja ndipo adapita kwa iye nakamufunsa kuti, “Udabwera ndi yani kuno? Ukuchita chiyani kuno? Ukugwira ntchito yanji kuno?” Iyeyo adaŵauza kuti, “Ndili pa chipangano ndi Mika, adandilemba ntchito ndipo ndine wansembe wake.” Iwo aja adamuuza kuti, “Chonde, tatifunsirako kwa Mulungu, kuti tidziŵe ngati ulendo wathu uno tiyende bwino.” Wansembeyo adaŵauza kuti, “Pitani ndi mtendere. Ulendo wanuwu Chauta akuuyang'anira.” Apo anthu asanu aja adachoka nakafika ku Laisi. Adakaona anthu amene ankakhala kumeneko, nazindikira kuti anthuwo ankakhala popanda choŵavuta, monga momwe ankakhalira Asidoni. Anali anthu aphee ndi opanda tcheru, osasoŵa kanthu kalikonse ndiponso anali anthu achuma. Adaona kuti anthuwo ankakhala kutali ndi Asidoni ndipo sankayenderana konse ndi anthu ena. Okazonda dziko aja atabwerera kwa abale ao ku Zora ndi ku Esitaoli, abale aowo adaŵafunsa kuti, “Nanga mutisimbira zotani?” Iwo adayankha kuti, “Fulumirani, tiyeni tikamenyane nawo nkhondo, pakuti dziko laolo taliwona, nlachonde kwambiri. Monga inu simuchitapo kanthu? Musachedwe kukaloŵa m'dzikomo ndi kukalilanda. Mukapita, mukaŵapeza kuti ndi anthu opanda tcheru. Dzikolo nlalikulu. Ndithudi Mulungu walipereka m'manja mwanu dziko limenelo. Malowo ngosasoŵa kanthu kalikonse kopezeka pa dziko lapansi.” Tsono anthu 600 a fuko la Dani adatenga zida zankhondo, nanyamuka ku Zora ndi ku Esitaoli. Adakamanga zithando zankhondo ku Kiriyati-Yearimu m'dziko la Yuda. Chifukwa cha chimenechi malowo akutchedwa zithando za Dani mpaka pano, ndipo ali kuzambwe kwa Kiriyati-Yearimu. Kuchokera kumeneko adapita ku dziko lamapiri la ku Efuremu, nakafika ku nyumba ya Mika. Tsono anthu asanu amene adaapita kukazonda dziko la Laisi aja adaŵafunsa abale aowo kuti, “Kodi mukudziŵa kuti imodzi mwa nyumba zimenezi muli chovala cha efodi, mafano am'nyumba, otchedwa terafimu, ndiponso fano losema ndi lina lachitsulo? Ndiye mudziŵa chochita.” Anthuwo adapatuka nakafika kunyumba kwa Mika, kumene mnyamata wachilevi uja ankakhala, nakamufunsa m'mene zinkamuyendera zinthu. Nthaŵi imeneyo nkuti anthu 600 a fuko la Dani okhala ndi zida zankhondo aja ataima pa khomo lapachipata. Apo anthu asanu amene adaali atazonda dziko aja adakaloŵa nakatenga fano losema lija, chovala cha efodi, mafano am'nyumba aja, ndi fano lachitsulo. M'menemo nkuti wansembe ataimirira pa khomo lapachipata pamodzi ndi anthu 600 okhala ndi zida zankhondo aja. Pamene anthuwo adakaloŵa m'nyumba ya Mika ndi kukatenga fano losema lija, chovala cha efodi, mafano am'nyumba ndi fano lachitsulo, wansembeyo adaŵafunsa kuti, “Kodi chikatere, ndiye kuti chiyani?” Iwo adamuyankha kuti, “Khala chete, usalankhule, tiye kuno, ukakhale mlangizi wathu ndi wansembe wathu. Kodi si kwabwino koposa kwa iwe kuti ukhale wansembe wa fuko lathunthu la Israele m'malo mokhala wansembe wa munthu mmodzi yekha?” Apo mtima wake wa wansembeyo udasangalala, ndipo adatenga chovala cha efodi, mafano am'nyumba, ndi fano losema lija, natsagana nawo anthuwo. Choncho adachoka napita, atatsogoza ana, ng'ombe ndiponso akatundu ao. Atapita kamtunda ndithu kuchokera pa nyumba ya Mika, Mikayo ndi anthu amene anali m'nyumba zoyandikana naye, adasonkhana kuti alondole anthu a fuko la Dani ndipo adaŵapeza. Iwowo adafuulira anthu a fuko la Dani aja ndipo anthu a fuko la Daniwo adatembenukira kumbuyo nafunsa Mika kuti, “Kodi chakuvuta nchiyani kuti uzibwera ndi chigulu chotere?” Mika adaŵayankha kuti, “Mwanditengera milungu yanga imene ine ndidapanga, mwandilandanso wansembe wanga nkumapita, nanga ine chanditsalira nchiyani? Ndiye inu mungandifunse kuti, ‘Kodi chakuvuta nchiyani?’ ” Anthu a fuko la Dani aja adayankha kuti, “Usaonjezenso mau ena, mwinamwina anthu aŵa apsa mtima nakumenya, ndipo iweyo ndi banja lako nonse muphedwa.” Tsono anthu a fuko la Dani aja adapita, ndipo pamene Mika adaona kuti anthuwo ngamphamvu kupambana iyeyo, adangobwerera kunyumba kwake. Atatenga zinthu zimene Mika adapanga zija pamodzi ndi wansembe wake uja, anthu a fuko la Daniwo adakafika ku Laisi kwa anthu aphee ndi opanda tcheru aja. Adaŵathira nkhondo naŵapha, nkutentha mzinda wao ndi moto. Kunalibe oŵapulumutsa, popeza kuti kunali kutali ndi ku Sidoni ndipo sankayenderana konse ndi anthu ena. Mzindawo unali m'chigwa cha ku Beterehobu. Anthu a fuko la Daniwo adamanganso mzindawo ndi kumakhalamo. Mzindawo adautcha Dani kutengera dzina la Dani kholo lao, amene anali mwana wa Israele. Koma dzina la mzindawo poyamba lidaali Laisi. Tsono anthu a fuko la Dani aja adaimiritsa fano la siliva wosungunula lija. Ndipo Yonatani, mwana wa Geresomo, mwana wa Mose, pamodzi ndi ana ake onse, adakhala ansembe a anthu a fuko la Dani mpaka pa tsiku la ukapolo wa dzikolo. Motero anthu a fuko la Dani aja ankapembedza fano lija limene Mika adapanga, nthaŵi yonse pamene chihema cha Mulungu chinali ku Silo. Masiku amenewo, pamene ku Israele kunalibe mfumu, munthu wina wachilevi ankakhala kutali ku dziko lamapiri la ku Efuremu. Iyeyo adakwatira mzikazi wa ku Betelehemu m'dziko la Yuda. Tsiku lina mzikazi wake uja adamkwiyira mwamunayo ndipo adathaŵa napita kwa bambo wake ku Betelehemu m'dziko la Yuda. Adakhala kumeneko miyezi inai. Tsono mwamuna wake adanyamuka namtsatira kuti akakambe naye mofatsa, kumpempha kuti abwerere. Mwamunayo anali ndi mtumiki wake ndi abulu ake aŵiri. Ndipo adafika ku nyumba ya bambo wake wa mkaziyo. Tsono mkaziyo adamloŵetsa m'nyumba ndipo bambo wake adamlandira ndi manja aŵiri. Mpongozi wakeyo, bambo wake wa mkazi uja, adamuuza kuti aswere, choncho adakhalako masiku atatu. Ankadya, namamwa ndi kumagona kumeneko. Tsiku lachinai lake iwo adadzuka m'mamaŵa, iye nkukonzeka kuti azipita. Koma bambo wake wa mkaziyo adauza mkamwini wake uja kuti, “Yambani mwadya chakudya, pambuyo pake mutha kupita.” Choncho anthu aŵiriwo adakhala pansi, nadya ndi kumwa limodzi. Bambo wa mkaziyo adauza mwamunayo kuti, “Gonaninso konkuno lero, musangalale.” Pamene munthuyo adanyamuka kuti azipita, mpongozi wake adamkakamiza kuti agonenso komweko. Tsiku lachisanu lake adadzuka m'mamaŵa kuti azipita. Bambo wake wa mkaziyo adamuuza kuti, “Yambani mwadya chakudya ndipo mudikire mpaka madzulo.” Choncho aŵiri onsewo adadyera limodzi. Pamene munthuyo ndi mzikazi wake ndiponso mtumiki wake adanyamuka kuti azipita, bambo wake wa mkaziyo adaŵauza kuti, “Onani, dzuŵa ndiye lapita, ndipo ano ndi madzulo. Gonaninso konkuno lero ndapota nanu. Onani kulikuda. Gonani konkuno, musangalale. Maŵa mudzuka m'mamaŵa nkumapita kwanu.” Koma munthu uja sadafune kugonanso tsiku limenelo. Mwakuti adanyamuka nkumapita, nakafika ku malo oyang'anana ndi Yebusi (ndiye kuti Yerusalemu). Iyeyo anali atatenga abulu aŵiri okhala ndi zishalo zake, ndipo mzikazi wake uja anali naye limodzi. Pamene ankayandikira ku Yebusi, nkuti kuli madzulo ndithu, ndipo mtumiki uja adauza mbuyake kuti, “Bwanji tsopano tingopatuka, kuloŵa mu mzinda wa Ayebusiwu ndi kukagona momwemo?” Mbuyake adayankha kuti, “Sitipatuka kuloŵa mu mzinda wa alendo amene sali Aisraele. Koma tipitirira mpaka ku Gibea.” Motero adauza mtumiki wakeyo kuti, “Tiye tikafike pafupi ndi malo ndatchulawo, ndipo tikagone ku Gibea kapena ku Rama.” Choncho adapitirira nayenda ulendo wao, ndipo dzuŵa lidaŵaloŵera atafika pafupi ndi Gibea, mzinda wa fuko la Benjamini. Adapatukira kumeneko kuti akaloŵe mu mzinda wa Gibea, ndi kugona komweko usiku umenewo. Adakaloŵa mumzindamo nakakhala pansi pa bwalo, pakuti panalibe munthu ndi mmodzi yemwe amene adaŵalandira kunyumba kwake, kuti apeze pogona. Kenaka adangoona munthu wina wokalamba akuchokera ku ntchito kumunda kwake madzulo. Anali wa ku dziko lamapiri la ku Efuremu, koma ankakhala nao ku Gibea. (Eni ake malowo anali Abenjamini). Munthu wokalamba uja atakweza maso adaona wapaulendo uja atakhala pa bwalo la mumzindamo, namufunsa kuti, “Kodi ulendowu, mukupita kuti? Nanga mukuchokera kuti?” Mlendoyo adayankha kuti, “Tikupita kutali ku dziko lamapiri la ku Efuremu kumene ndimakhala, ndipo tikuchokera ku Betelehemu ku dziko la Yuda. Ndidaapita ku Betelehemu ndipo tsopano ndikupita kwathu, koma palibe ndi mmodzi yemwe wondilandira m'nyumba mwake. Tili nawo udzu ndi chakudya cha abulu athu. Ndili nayenso buledi ndi vinyo wondikwanira ine, mdzakazi wangayu, ndi mtumiki amene ali ndi ifeyu. Palibe chimene tikusoŵa.” Apo munthu wokalambayo adati, “Mtendere ukhale nanu. Ndikuthandizani pa zosoŵa zanu zonse, koma tsono musagone pa bwalo usiku uno.” Choncho adapita nawo kunyumba kwake, naŵapatsa chakudya abulu aja. Ndipo alendowo adasamba mapazi ao, nalandira chakudya ndi chakumwa. Pamene anali kudya mosangalala, adangoona anthu amumzindamo, anthu achabechabe, ataizinga nyumbayo, namamenya chitseko. Adauza munthu wokalamba uja, mwini wake wa nyumbayo, kuti, “Mtulutse munthu uja wabwera m'nyumba mwakoyu, tiseŵere naye.” Mwini wake wa nyumba uja adatuluka nakaŵauza kuti, “Iyai, abale anga, musachite zoipa zotere. Munthuyu wabwera m'nyumba mwanga muno, musachite chinthu chonyansa chotere. Onani pano pali mwana wanga wanamwali wosamdziŵa mwamuna pamodzi ndi mzikazi wa mlendoyu. Ndikutulutsireni ameneŵa tsopano lino, muŵatenge ndipo muchite nawo zimene mufuna. Koma musachite chinthu chonyansa ndi mlendoyu.” Koma anthuwo sadafune kumumvera. Choncho mlendo uja adagwira mzikazi wake uja namtulutsira kunali iwoko, iwowo nkugona naye, nachita naye zoipa usiku wonse mpaka m'maŵa. M'bandakucha adamlola kuti apite. Ndipo m'maŵa kulikucha, mkaziyo adabwera nagwa pansi pakhomo pa nyumba ya munthu uja m'mene munali mwamuna wake muja. Adakhala pamenepo ali thasa mpaka kudayera. Mwamuna wakeyo adadzuka m'maŵa, ndipo atatsekula zitseko za nyumba kuti azipita, anangoona mzikazi wake uja ali thasa pakhomo pa nyumba, manja ake ali pa chiwundo. Adamuuza kuti, “Dzuka tizipita.” Koma mkaziyo sadayankhe kanthu. Tsono adamkweza pabulu, ndipo mlendoyo adanyamuka kupita kwao. Ataloŵa m'nyumba mwake, adatenga mpeni, naduladula thupi la mkaziyo m'nthuli khumi ndi ziŵiri. Ndipo adazitumiza m'dziko lonse la Israele. Onse amene adaona zimenezi ankati, “Zoterezi sizinachitikepo kuyambira nthaŵi imene Aisraele adatuluka m'dziko la Ejipito mpaka lero lino. Tiziganize bwino ndipo tipangane ndi kuchitapo kanthu.” Aisraele onse adanyamuka kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba, kudzanso dziko la Giliyadi, ndipo adasonkhana pamaso pa Chauta ku Mizipa. Atsogoleri a anthu onse ndi a mafuko onse a Aisraele adabwera ku msonkhano wa anthu a Mulungu. Onse pamodzi analipo 400,000 oyenda pansi omenya nkhondo ndi lupanga. M'menemo nkuti anthu a fuko la Benjamini atamva kuti Aisraele apita ku Mizipa. Tsono Aisraele adati, “Tiwuze, kodi zoipa zoterezi zachitika bwanji?” Apo Mlevi uja, mwamuna wa mkazi wophedwayo, adati, “Ndidafika ku Gibea, mzinda wa Abenjamini, ineyo ndi mzikazi wanga, kuti tigone kumeneko. Anthu a ku Gibea adandiwukira nazinga nyumba imene munali ine nthaŵi ya usiku. Ankafuna kundipha ndipo adamchita zoipa mzikazi wangayo mwakhakhamizo mpaka iye adafa. Ndidamtenga mzikaziyo ndi kumduladula nthulinthuli, nkuzitumiza kwa fuko lililonse la Aisraele. Ndithudi anthu amene aja achita zinthu zonyansa ndi zoipa kwabasi m'dziko lino la Israele. Nzimenezotu, inu Aisraele, ndikuuza nonsenu, mupereke malangizo anu ndipo mupangane pompano.” Anthu onse adadzuka pamodzi nati, “Palibe munthu ndi mmodzi yemwe mwa ife amene apite ku hema lake, palibe amene abwerere kunyumba kwake. Koma tsono zimene tiŵachite anthu a ku Gibea ndi izi: tipita kukalimbana nawo mzindawo potsata zimene maere atiwuze. M'mafuko onse a Aisraele tisankhula anthu khumi pa anthu 100 aliwonse. Ameneŵa adzasonkhanitsa zakudya za ankhondo, ndipo ankhondowo adzapita kukalipsira anthu a ku Gibea, mzinda wa ku Benjamini, chifukwa cha tchimo lao lonyansa zedi limene adachita m'dziko la Israele.” Motero Aisraele onse adasonkhana atagwirizana chimodzi pofuna kulimbana nawo mzindawo. Mafuko a Aisraele adatuma anthu kwa fuko lonse la Benjamini, kuti akafunse kuti, “Kodi zoipa zimene mwachita pakati panupazi nzotani? Ndiye ife tsopano tikuti mubwere nawo anthuwo, anthu achabechabe aja a ku Gibea, kuti tiŵaphe, kuti potero tichotse kulaulaku m'dziko la Israele.” Koma Abenjamini sadafune kumva mau a Aisraele, abale ao. Choncho Abenjamini onse adatuluka m'mizinda yao ku Gibea kukamenyana nkhondo ndi Aisraele. Tsiku limenelo Abenjamini adasonkhanitsa ankhondo 26,000, osaŵerenga anthu ena a ku Gibea 700 osankhidwa. Mwa anthu onseŵa panali anthu 700 amanzere, amene ankatha kulasa ndi mwala ngakhale tsitsi limodzi, osaphonya konse. Aisraele onse, kupatula Abenjamini, adasonkhanitsa anthu amalupanga 400,000, anthu ake odziŵa bwino nkhondo. Aisraele adanyamuka napita ku Betele kukafunsa kwa Mulungu kuti, “Ndani mwa ife amene ayambe kukamenyana nkhondo ndi Abenjamini?” Chauta adayankha kuti, “Fuko la Yuda ndilo limene liyambe.” Tsono Aisraele adadzuka m'maŵa nakamanga zithando zao moyang'anana ndi Gibea. Aisraele adapita kukamenyana nkhondo ndi Abenjamini, nakhazika ankhondo ao kuyang'ana mzinda wa Gibea. Nawonso Abenjamini adatuluka ku Gibea ndipo tsiku limenelo adapha Aisraele 22,000. Koma Aisraelewo adalimbitsana mtima ndipo adakhazika ankhondo ao kachiŵiri pa malo omwe aja pamene adaaŵakhazika tsiku loyamba lija. Tsono Aisraelewo adapita kukalira pamaso pa Chauta mpaka madzulo. Adakafunsa Chauta kuti, “Kodi tipitenso kachiŵiri kukamenyana nawo nkhondo Abenjamini, abale athu?” Chauta adayankha kuti, “Inde pitani mukamenyane nawo.” Choncho Aisraele adafika pafupi, kuti akalimbane ndi Abenjamini tsiku lachiŵiri lake. Abenjamini adatulukanso mu mzinda wa Gibea, kukalimbana nawo tsiku lachiŵirilo, ndipo adapha ankhondo a Aisraele 18,000. Tsono Aisraele onse, ndiye kuti gulu lonse la ankhondo, adapita ku Betele ndi kukalira kumeneko. Adakhala pansi pamaso pa Chauta, nasala chakudya tsiku limenelo mpaka madzulo, ndipo adapereka nsembe zopsereza ndi zamtendere pamaso pa Chauta. Bokosi lachipangano la Chauta linali kumeneko masiku amenewo. Finehasi mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni, ndiye ankayang'anira bokosilo masiku amenewo. Choncho Aisraele adafunsa Chauta kuti, “Kodi tipitenso kukamenyana nawo nkhondo Abenjamini, abale athu, kapena tingoleka?” Chauta adayankha kuti, “Pitaninso, pakuti maŵa ndidzaŵapereka m'manja mwanu.” Choncho Aisraele adaika anthu obisalira mozungulira mzinda wa Gibea. Adapita kukamenyana ndi Abenjamini tsiku lachitatu lake, nakhazika ankhondo ao kuti athire nkhondo mzinda wa Gibea monga masiku ena aja. Abenjamini nawonso adatuluka kukamenyana nawo anthuwo, napita chapatali ndithu ndi mzindawo. Ndipo monga mwa masiku onse, adayamba kuŵamenya koopsa ndi kupha Aisraele makumi atatu amene anali m'miseu yaikulu, ena mu mseu waukulu wa ku Betele, ena mu mseu waukulu wa ku Gibea ndiponso ena kwina koyera. Ndipo adati, “Taŵapirikitsa monga poyamba paja.” Koma Aisraele adati, “Tiyeni tithaŵe kuti apite ku miseu chapatali ndithu ndi mzinda wao.” Choncho Aisraelewo adanyamuka m'malo ao, nakandanda ku Baala-Tamara. Pamenepo Aisraele amene adaabisalira aja adatuluka m'malo ao kuzambwe kwa Geba. Aisraele osankhidwa amene adabwera kudzalimbana ndi mzinda wa Gibea analipo 10,000, ndipo nkhondo idalimba kumeneko. Koma Abenjamini sankadziŵa kuti zoopsa zili pafupi kuŵagwera. Tsono Chauta adagonjetsa Abenjamini pamaso pa Aisraele, ndipo Aisraelewo adaononga ankhondo a Abenjamini okwanira 25,100 tsiku limenelo. Motero Abenjamini adaona kuti agonjetsedwa. Paja gulu lalikulu la Aisraele lidaathaŵa Abenjamini chifukwa linkadalira anthu aja amene lidaaŵaika kuti abisalire mzinda wa Gibea. Apo anthu obisalira aja adafulumira kuuthira nkhondo mzinda wa Gibeawo. Adapha anthu onse amumzindamo ndi lupanga. Tsono chizindikiro chimene adaapangana Aisraele a gulu lalikulu ndi anthu obisalira aja chinali chakuti, akafukiza utsi wambiri ngati mtambo mumzindamo, Aisraele ambiriwo abwerere kudzamenya nkhondo. M'menemo nkuti Abenjamini atayamba kuŵamenya Aisraelewo koopsa ndi kupha anthu makumi atatu. Iwo ankati, “Ndithu, taŵapha monga poyamba paja.” Koma pamene utsi wachizindikiro uja udayamba kuti tolotolo kukwera kumwamba mumzindamo, Abenjamini adayang'ana kumbuyo, nkuwona mu mzinda wonsewo utsi uli tolotolo kukwera kumwamba. Pomwepo Aisraele adabwerera ndipo Abenjamini adayamba kuwopa ndi kutaya mtima, pakuti adaaona kuti zoopsa zili pafupi kuŵagwera. Nchifukwa chake Abenjamini adayamba kuthaŵa Aisraelewo, naloŵa njira ya ku dondo. Koma nkhondo idaŵapeza, ndipo adaphedwa ndi Aisraele amene ankatuluka mu mzinda. Adaŵazinga Abenjaminiwo naŵapirikitsa ndi kuŵaonongeratu osaŵachitira chifundo mpaka ku dera la Gibea kuvuma kwake. Abenjamini amene adaphedwa analipo 18,000. Onsewo anali anthu olimba mtima kwambiri. Anthu amene adatsalira, adatembenuka nathaŵira ku dondo ku thanthwe la Rimoni. Mwa iwowo anthu 5,000 adaphedwa m'miseu yaikulu. Adaŵapirikitsabe Abenjaminiwo mkaka ku Gidomu, naphanso enanso 2,000. Choncho Abenjamini onse amene adafa tsiku limenelo adakwanira ankhondo 25,000. Onsewo anali anthu olimba mtima kwambiri. Koma anthu 600 okha adakafika ku dondo ku thanthwe la Rimoni, nakakhala ku thanthwe la Rimoniko miyezi inai. Tsono Aisraele adabwerera m'mbuyo kukamenyana ndi Abenjamini otsala, naŵapha ndi lupanga, anthu ndi nyama zomwe, pamodzi ndi zonse zimene adakumana nazo. Ndipo adatentha mizinda yonse imene adaipeza. Aisraele anali atalumbira ku Mizipa kuti, “Palibe ndi mmodzi yemwe mwa ife amene adzapereke mwana wake wamkazi kuti akwatiwe ndi Abenjamini.” Anthuwo adafika ku Betele, nakhala pansi kumeneko pamaso pa Mulungu mpaka madzulo, ndipo adafuula nalira ndi chisoni chambiri. Iwowo ankati, “Chauta, Mulungu wa Aisraele, chifukwa chiyani zimenezi zachitika m'dziko la Aisraele, kuti lero fuko la Benjamini lilipafupi kuchotsedwa m'dziko la Israele?” M'maŵa mwake anthuwo adadzuka m'mamaŵa. Adamanga guwa kumeneko, napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zamtendere. Aisraele adati, “Kodi ndani pakati pa mafuko a Aisraele amene sadafike ku msonkhano wa Chauta?” Paja anali atachita malumbiro aakulu okhudza munthu amene sadapite kwa Chauta ku Mizipa kuti, “Munthu wotero ayenera kuphedwa.” Koma Aisraele adamvera chifundo abale ao a fuko la Benjamini nati, “Fuko limodzi lachotsedwa m'dziko la Israele lero lino. Kodi tidzaŵapezera kuti akazi anthu amene atsaliraŵa, popeza kuti talumbira kwa Chauta kuti sitidzaŵapatsa ana athu aakazi kuti aŵakwatire?” Tsono iwowo adafunsa kuti, “Kodi m'fuko la Aisraele ndani amene sadabwere kwa Chauta ku Mizipa?” Tsono kudapezeka kuti panalibe ndi mmodzi yemwe wa ku Yabesi-Giliyadi amene adabwera ku msonkhano kuzithando kuja. Pakuti m'mene anthu ankasonkhana, adangoona kuti palibe munthu ndi mmodzi yemwe wa ku Yabesi-Giliyadi. Choncho mpingo udatumiza kumeneko anthu 12,000 mwa anthu ao, olimba kwambiri, naŵalamula kuti, “Pitani mukaŵaphe anthu a ku Yabesi-Giliyadi ndi lupanga. Mukaphenso akazi ndi ana omwe. Zimene mukachite ndi izi, ‘Mukaphe amuna onse ndiponso mkazi aliyense amene adadziŵapo kale mwamuna.’ ” Pakati pa anthu a ku Yabesi-Giliyadi adapeza anamwali 400 amene sadadziŵepo amuna. Amenewo adabwera nawo ku zithando ku Silo, mzinda umene uli m'dziko la Kanani. Pamenepo mpingo wonse udatumiza uthenga kwa Abenjamini amene anali ku thanthwe la ku Rimoni kukaŵauza kuti nkhondo yatha. Abenjamini adabwera nthaŵi imeneyo. Ndipo Aisraele adaŵapatsa Abenjaminiwo akazi a ku Yabesi-Giliyadi amene sadaŵaphe aja. Koma adapereŵera, osakwanira. Aisraele adaŵamvera chifundo Abenjaminiwo chifukwa chakuti Chauta anali atachotsako anthu ena mu fuko limodzi la Aisraele. Tsono akuluakulu a mpingo adati, “Kodi tikaŵapezera kuti akazi anthu amene atsaliraŵa, popeza kuti akazi a fuko la Benjamini adaphedwa?” Iwowo adati, “Nkofunika kuti anthu otsalira a fuko la Benjamini akhale nazo zidzukulu, kuti fuko lao lisafafanizike pa mtundu wa Israele. Komabe sitingathe kuŵapatsa ana athu aakazi kuti aŵakwatire.” Paja Aisraele anali atalumbira kuti, “Akhale wotembereredwa munthu amene apatse Mbenjamini mkazi.” Choncho adati, “Paja kuli chikondwerero cha chaka ndi chaka cholemekeza Chauta ku mzinda wa Silo.” Silo ali kumpoto kwa Betele, kuvuma kwa Lebona. Ndiye adalamula Abenjamini aja kuti, “Pitani mukabisale m'minda yamphesa, ndipo muzikapenyetsetsa. Ana aakazi a ku Silo akamakabwera kudzavina magule, pomwepo mutuluke m'minda yamphesa ndi kukaŵagwira, aliyense wake, nkupita nawo ku dziko la Benjamini. Tsono pamene azibambo kapena alongo ao adzabwere kuno kudzadandaula, ife tidzaŵauza kuti, ‘Chonde, tiloleni kuti tiŵatenge, popeza kuti anthuŵa sitidaŵapezere akazi pomenya nkhondo, ndipo inunso simudachita kuŵapatsa akaziwo. Mukadatero bwenzi tsopano mutapalamula.’ ” Abenjaminiwo adachitadi zimenezi. Mwa akazi amene ankavina aja adatengapo ao, molingana ndi chiŵerengero chao, napita nawo. Kenaka adanyamuka kubwerera ku dziko lakwao nakamanganso mizinda yatsopano ndi kumakhalamo. Tsono Aisraele adachoka kumeneko nthaŵi yomweyo, napita aliyense ku fuko lake ndiponso ku banja lake, ndipo kuchokera kumeneko aliyense adapita ku dera la choloŵa chake. Masiku amenewo kunalibe mfumu ku Israele. Munthu aliyense ankangochita zimene zinkakomera mwiniwakeyo. Nthaŵi ina, pamene aweruzi ankalamulira Israele, mudaagwa njala m'dzikomo. Tsono munthu wina wa ku Betelehemu m'dziko la Yuda, adapita ndi mkazi wake ndi ana ake aŵiri, kukakhala nao mwakanthaŵi ku dziko la Mowabu. Munthuyo anali Elimeleki, mkazi wake anali Naomi. Ana ake aŵiriwo anali Maloni ndi Kiliyoni. Onsewo anali Aefurati a ku Betelehemu m'dziko la Yuda, koma adapita ku Mowabu nakhala komweko. Tsono Elimeleki mwamuna wa Naomi adamwalira, ndipo Naomiyo adatsala ndi ana aŵiri aja. Iwoŵa adakwatira akazi achimowabu. Wina dzina lake anali Olipa, winayo anali Rute. Adakhala ku Mowabuko pafupi zaka khumi. Koma Maloni ndi Kiliyoni adamwalira, kotero kuti Naomi adataya ana ake aŵiri aja, pamodzi ndi mwamuna wake yemwe. Pamenepo mkaziyo ndi apongozi ake aŵiri aja adayamba kukonza ulendo wobwerera kwao kuchokera ku Mowabu, poti anali atamva ku Mowabuko kuti Chauta adadalitsa anthu ake ndi kuŵapatsa chakudya. Choncho adanyamuka, pamodzi ndi apongozi akewo, kuchoka kumene ankakhala kuja, nayamba ulendo wobwerera ku dziko la Yuda. Tsono Naomi adauza apongozi ake aŵiri aja kuti, “Pitani, aliyense abwerere kwa mai wake. Chauta akuchitireni zabwino, monga momwe mudachitira malemu aja ndi ine ndemwe. Chauta akuthandizeni kuti mupeze pokhala, ndipo aliyense mwa inu akwatiwe.” Pompo adaŵampsompsona. Koma iwo adayamba kulira mokweza, nauza Naomiyo kuti, “Iyai, ife tipita nao kwa anthu akwanu.” Koma Naomi adaŵauza kuti, “Pepani ana anga, bwererani kwanu. Chifukwa chiyani mukufuna kupita nao? Kodi mukuganiza kuti ndingathe kubala ana ena aamuna, kuti adzakhale amuna anu? Bwererani ana anga, muzipita kwanu, pakuti ndakalamba kwambiri, sindingathenso kukhala ndi mwamuna. Ngakhale ndikadanena kuti chikhulupiriro chilipobe, ngakhale ndikadakhala ndi mwamuna usiku uno, kuti ndibale ana aamuna, kodi tsono mukadatha kudikira mpaka akule? Kodi zimenezi zikadakuletsani kukwatiwa? Ai, ana anga, zotere zikadandiŵaŵa kwambiri chifukwa cha inu, poona kuti sindinu koma ndine amene Chauta adafuna kuti ndizunzike.” Pamenepo iwo aja adayambanso kulira mokweza. Olipa adampsompsona mpongozi wake ndi kumulaŵira, koma Rute adakangamira Naomiyo. Tsono Naomi adauza Rute kuti, “Ona, mbale wako wabwerera kwao ndi kwa milungu yake. Nawenso bwerera, umulondole mbale wakoyo.” Koma Rute adamuuza kuti, “Musandiwumirize kuti ndikusiyeni kapena kuti ndisakutsateni. Kumene mupite inuko, inenso ndipita komweko, ndipo kumene mukakhale inuko, inenso ndikakhala komweko. Abale anu adzakhala abale anga, ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga. Kumene inu mukafere, inenso ndikafera komweko ndi kuikidwa komweko. Chauta andichite choipa chilichonse chingakule motani, ngati kanthu kena kalikonse katisiyanitse, kupatula imfa.” Naomi ataona kuti Rute watsimikiza kupita nao, sadanenenso kanthu. Choncho aŵiriwo adapitirira ulendo wao, mpaka adakafika ku Betelehemu. Akaziwo atafika ku Betelehemuko, anthu onse am'mudzimo adatekeseka chifukwa cha iwowo. Tsono akazi ena ankati, “Kodi ameneyu ndi Naomi?” Iyeyo adaŵauza kuti, “Musamanditchule Naomi, koma muzinditchula Mara, poti Mphambe wandizunza kwambiri. Ndidaapita ndili ndi zinthu zambiri, koma Chauta wandibweza ndili wopanda kanthu. Motero munditchulirenji Naomi pamene Mphambe wandisautsa ndi kundigwetsera mavuto oŵaŵa?” Umu ndi m'mene Naomi adabwerera kuchokera ku Mowabu pamodzi ndi Rute mpongozi wake wachimowabu uja. Ndipo adafika ku Betelehemu pa nthaŵi yoyamba kudula barele. Naomi anali ndi wachibale wake wachuma kwambiri, wa m'banja la malemu mwamuna wake uja Elimeleki, dzina lake Bowazi. Tsiku lina Rute adauza Naomi kuti, “Mundilole kuti ndikakunkhe barele ku munda wa munthu aliyense amene akandikomere mtima.” Naomi adamuuza kuti, “Pita mwana wanga.” Choncho Rute adanyamuka napita kukakunkha ku minda, anthu atakolola kale. Kudangochitika kuti adakafika ku munda wa Bowazi amene anali wa m'banja la Elimeleki. Posachedwa Bowazi adafika kuchokera ku Betelehemu, ndipo adalonjera anthu okolola aja kuti, “Chauta akhale nanu.” Iwo adayankha kuti, “Chauta akudalitseni.” Tsono Bowazi adafunsa kapitao wake amene ankayang'anira anthu okolola aja kuti, “Kodi mai uyu ndani?” Kapitao wakeyo adayankha kuti, “Maiyu ndi Mmowabu amene adabwera ndi Naomi kuchokera ku dziko la Mowabu. Iyeyu wandipempha kuti, ‘Chonde mundilole kuti ndikunkheko barele m'munda m'mene anthu akolola kale!’ Choncho wakhala akukunkha kuyambira m'mamaŵa mpaka tsopano lino, osapuma ndi pang'ono pomwe.” Apo Bowazi adauza Rute kuti, “Tamvera, mwana wanga, usapite kukakunkha ku munda wina, usasiye munda uno, koma uzitsata adzakazi angaŵa. Uziyang'ana munda akukololawu, ndipo uziŵatsata pambuyo. Ndaŵauza anyamatawo kuti asakuvute. Tsono ukamamva ludzu, uzipita ku mitsuko ndi kukamwa madzi amene anyamatawo atunga.” Rute adaŵerama, nazyolikitsa nkhope pansi, ndipo adafunsa kuti, “Chifukwa chiyani ndapeza kukoma mtima kotereku mwa inu, kuti mulabadeko za ine mlendo?” Koma Bowazi adayankha kuti, “Zonse zimene wakhala ukuchitira mpongozi wako, kuyambira nthaŵi imene mwamuna wako adamwalira, ndazimva zonsezo. Ndamvanso kuti udasiya bambo wako, mai wako ndi dziko lako, ndipo wabwera kwa anthu amene sudaŵadziŵe ndi kale lonse. Chauta akubwezere zabwino zimene wachitazi. Akupatse mphotho yaikulu Chauta, Mulungu wa Aisraele, poti wabwera kwa Iye kuti akuteteze.” Apo Rute adati, “Mwandikomera mtima kwambiri mbuyanga, mwandisangalatsa ndipo mwandilankhula mwachifundo, ngakhale sindine mmodzi mwa adzakazi anu.” Nthaŵi yakudya Bowazi adauza Rute kuti, “Bwera kuno, udzadyeko buledi ndi kusunsa nthongo yako m'vinyo.” Choncho adakhala pansi pafupi ndi anthu okolola aja, ndipo adampatsa barele wokazinga. Adadya mpaka kukhuta ndipo barele wina adatsalako. Pamene adanyamuka mkaziyo kuti akakunkhe, Bowazi adaŵalangiza antchito ake aja kuti, “Muzimulola mkaziyu kuti azikunkha ngakhale pakati pa mitolo, osamchititsa manyazi. Muzimusololerako ngala zina zam'mitolo ndi kumlekera kuti azikunkha, osamdzudzula.” Choncho Rute adakunkha m'mundamo mpaka madzulo. Pambuyo pake adapuntha barele amene adakunkha uja, ndipo adakwanira pafupi makilogramu khumi. Adatenga bareleyo kupita naye ku mudzi, nakaonetsa mpongozi wake. Atatero, adatulutsa chakudya chimene chidatsalira atakhuta chija, napatsa mpongozi wakeyo. Naomi adamufunsa kuti, “Unakakunkha kuti lero? Unakagwira ntchitoyi m'munda mwa yani? Ngwodala munthu amene anakukomera mtimayo.” Rute adauza mpongozi wake za munthu amene adagwirako ntchito, adati, “Munthuyo dzina lake ndi Bowazi.” Apo Naomi adauza Rute kuti, “Munthu ameneyo amdalitse Chauta, amene amasunga malonjezo ake kwa anthu amoyo, ngakhalenso kwa anthu akufa.” Ndipo adatinso, “Munthuyo ndi mnansi wathu, mmodzi mwa achibale athu, amene ali ndi udindo wotisamala.” Tsono Rute Mmowabuyo adati, “Kuwonjezera pamenepo, munthuyo anandiwuza kuti, ‘Uzitsata antchito angaŵa mpaka atamaliza munda wanga kukolola.’ ” Naomi adauza Rute kuti, “Kuli bwino mwana wanga kuti uzipita ndi adzakazi ake, kuwopa kuti ukapita m'munda wina, angakuvute.” Motero Rute ankatsatira adzakazi a Bowaziwo, namakunkha, mpaka anthu atamaliza kudula barele ndi tirigu. Monsemo Rute ankakhala ndi mpongozi wakeyo. Tsiku lina Naomi adafunsa Rute kuti, “Kodi iwe mwana wanga, nanga sikwabwino kuti ndikupezere pokhala, kuti zinthu zizikuyendera bwino? Bowazi amene adzakazi ake unali nawo, ndi wachibale wathu. Usiku uno iye akhala akupuntha barele ku malo ake opunthira. Samba tsono, udzole mafuta ndipo uvale zovala zabwino kwambiri, upite kopunthirako. Koma munthuyo asakakuzindikire mpaka atamaliza kudya ndi kumwa. Pamene akukagona, ukaonetsetse malo amene akagonewo. Tsono ukavundukule chofunda chake nukagona ku mapazi ake. Motero iyeyo akakuuza zoti uchite.” Rute adayankha kuti, “Zonse mwanenazi ndichita.” Choncho Rute adapita kopunthira kuja, ndipo adakachitadi monga momwe mpongozi wake uja adaamuuzira. Bowazi atamaliza kudya ndi kumwa, anali wosangalala, ndipo adapita kukagona pambali pa mulu wa barele. Tsono Rute adabwera mopanda mtswatswa, adavundukula mapazi a Bowazi, nagona pomwepo. Tsono pakati pa usiku Bowazi adadzidzimuka natembenuka, naona mkazi atagona ku mapazi ake. Adafunsa kuti, “Ndiwe yani?” Mkaziyo adayankha kuti, “Ndine Rute mdzakazi wanu. Popeza kuti ndinu wachibale, muyenera kundiwombola pakundiloŵa chokolo.” Apo Bowazi adati, “Chauta akudalitse, mwana wanga. Zabwino wachita potsirizazi zikupambana zoyamba zija zimene udachitira mpongozi wako, poti sudapite kwa anyamata osauka kapena olemera. Tsopano usadandaule, mwana wanga. Ndidzakuchitira zonse zimene upemphe, pakuti anzanga am'mudzimu akudziŵa kuti ndiwe mkazi wabwino. Nzoona, ine ndine wachibale, komabe alipo wachibale weniweni kupambana ine. Gona konkuno usiku uno mpaka m'maŵa. Ngati iyeyo adzakuloŵe chokolo, chabwino aloŵe. Koma ngati safuna, ndidzakuloŵa ndine, ndikulumbira pamaso pa Chauta wamoyo. Gona mpaka m'maŵa.” Choncho Rute adagona ku mapazi a Bowazi mpaka m'maŵa, koma adadzuka kudakali kamdimabe, chifukwa Bowaziyo sankafuna kuti anthu adziŵe kuti mkaziyo adaabwera kopunthira bareleko. Tsono Bowazi adauza Rute kuti, “Bwera nacho kuno chofunda wavalacho, uchiyale pansi.” Rute adayala chofundacho, ndipo Bowazi adayesa makilogramu makumi aŵiri a barele, namsenzetsa Rute uja. Tsono Rute adachoka nakaloŵa mu mzinda. Atafika kwa mpongozi wake uja, mpongoziyo adati, “Zinthu zakuyendera bwanji, mwana wanga?” Rute adamfotokozera zonse zimene munthu uja adamchitira, ndipo adati, “Wandipatsa makilogramu makumi aŵiri a barele, nandiwuza kuti, ‘Usapite kwa apongozi ako chimanjamanja.’ ” Apongozi akewo adayankha kuti, “Dikira mwana wanga, tiwone m'mene zikhalire zinthu, chifukwa munthuyo salekera pomwepo, koma azikonza zimenezi lero.” Nthaŵi yomweyo Bowazi adapita ku chipata cha mzinda nakakhala pansi, pa bwalo losonkhanirana. Tsono adangoona wachibale ankanena uja akufika. Apo Bowazi adati, “Bwenzi langa, tapatukira kuno, ukhale pansi apa.” Munthu uja adapatuka nakhala pansi. Adaitananso atsogoleri khumi amumzindamo naŵauza kuti, “Takhalani pansi apa.” Iwo adakhala pansi. Tsono adauza munthu wachibale uja kuti, “Naomi amene wabwerera kuchokera ku dziko la Mowabu, akugulitsa munda umene udaali wa malemu Elimeleki, wachibale wathu. Choncho ndinaganiza zokuuza zimenezi, kuti ugule mundawo pamaso pa anthu amene ali panoŵa, ndi pamaso pa atsogoleri a abale athu. Ngati ufuna kugula, ugule. Koma ngati sufuna, undiwuze kuti ndidziŵe, pakuti palibe wina woti augule koma iweyo, ndipo pambuyo pa iwe pali ine.” Munthuyo adati, “Ndigula munda umenewo.” Tsono Bowazi adamuuza kuti, “Tsiku limene udzagule mundawo kwa Naomi, udzatenganso Rute Mmowabu, mai wamasiye uja, kuti dzina la malemu aja lisungike pa choloŵa chao.” Apo wachibaleyo adati, “Sindingathe kugula mundawo kuti ukhale wanga, kuwopa kuti ndingaononge choloŵa changa. Mugule ndinu, ine sindingathe.” Masiku amenewo, munthu akamachita malonda kapena kusinthana kanthu ndi mnzake, zinkayenda motere: ankavula nsapato imodzi napatsa mnzakeyo. Imeneyi ndiyo inali njira yochitira umboni m'dziko la Israele. Choncho pamene wachibale uja adauza Bowazi kuti, “Gulani ndinu mundawo,” adavula nsapato yake napatsa Bowazi. Tsono Bowazi adauza atsogoleri ndi anthu onse aja kuti, “Nonsenu ndinu mboni lero, kuti ine ndagula kwa Naomi zonse zimene zidaali za malemu Elimeleki, ndiponso zonse za malemu Kiliyoni ndi za malemu Maloni. Ndatenganso Rute Mmowabu uja, mkazi wa malemu Maloni, kuti akhale mkazi wanga, kuti dzina la malemulo lisungike pa choloŵa chake, ndipo lisafafanizike pakati pa abale ake ndiponso m'mudzi mwake. Nonsenu ndinu mboni lero lino.” Apo anthu onse amene anali pachipata paja, pamodzi ndi atsogoleri aja, adati, “Inde, ndife mboni. Mkazi amene akudzaloŵa m'nyumba mwakoyo, Chauta amsandutse wofanafana ndi Rakele ndi Leya, akazi amene adamanga banja la Israele pombalira ana ambiri. Ukhale munthu wosasoŵa kanthu mu mzinda wa Efurata, ndipo ukhale munthu wotchuka mu mzinda wa Betelehemu. Ana ako amene Chauta adzakupatse mwa mai ameneyu, adzamange banja longa la Perezi, amene Tamara adabalira Yuda.” Choncho Bowazi adakwatira Rute, ndipo Chauta adadalitsa Ruteyo, mwakuti adatenga pathupi nabala mwana wamwamuna. Tsono akazi adauza Naomi kuti, “Ngwodala Chauta amene sadakusiyeni nokha opanda wachibale. Mwanayo dzina lake litchuke mu Israele. Mwanayo adzakupatsani moyo watsopano ndipo adzakuchirikizani mu ukalamba wanu. Inde wakubalirani mwana mpongozi wanu amene amakukondani, amene wakuwonetsani kuti akupambana ana aamuna asanu ndi aŵiri.” Naomi adanyamula mwanayo namfukata ndipo adakhala mlezi wake. Akazi achinansi ake adalengeza kuti, “Mwana wabadwa kwa Naomi.” Ndipo adamutcha dzina loti Obedi. Iyeyu adakhala bambo wake wa Yese, bambo wa Davide. Tsono zidzukulu za Perezi ndi izi: Perezi adabereka Hezironi, Hezironi adabereka Ramu, Ramu adabereka Aminadabu. Aminadabu adabereka Nasoni, Nasoni adabereka Salimoni. Salimoni adabereka Bowazi, Bowazi adabereka Obedi. Obedi adabereka Yese ndipo Yese adabereka Davide. Padaali munthu wina dzina lake Elikana, wa ku Ramataimu-Zofimu ku dziko lamapiri la Efuremu. Anali mwana wa Yerohamu, mwana wa Elihu, mwana wa Tohu, mwana wa Zufu, wa fuko la Efuremu. Elikanayo anali wamitala, mkazi wina dzina lake anali Hana, winayo anali Penina. Penina anali ndi ana, koma Hana analibe. Chaka ndi chaka Elikana ankapita ku Silo kuchokera ku mzinda kwao, kukapembedza ndi kukapereka nsembe kwa Chauta Wamphamvuzonse. Ku Siloko kunali ana aŵiri a Eli, Hofeni ndi Finehasi, amene anali ansembe a Chauta. Tsiku limene Elikana ankapereka nsembe, ankapatsako magawo a nsembeyo kwa mkazi wake Penina ndi kwa ana ake aamuna ndi aakazi. Ndipo ngakhale ankakonda Hana, ankangompatsa gawo limodzi chifukwa choti Chauta sadampatse ana. Tsono chifukwa choti Chauta sadampatse ana, mkazi mnzake uja ankangomnyodola ndi kumpeputsa, kuti amkwiyitse. Zimenezi zinkachitika chaka ndi chaka. Nthaŵi zonse akamapita ku nyumba ya Chauta, mkazi mnzakeyo ankamputa. Nchifukwa chake Hana ankangolira, ndipo sankafuna ndi kudya komwe. Mwina Elikana mwamuna wake ankamufunsa kuti, “Hana, kodi watani apa ukulira ndi kuwoneka wachisoni ndiponso sukufuna kudya? Kodi kwa iwe ineyo sindikuposa ana aamuna khumi?” Tsiku lina iwo atatha kudya ku Silo kuja, Hana adaimirira nakapemphera. Nthaŵi imeneyo nkuti Eli, wansembe uja, ali pa mpando pambali pa khomo la Nyumba ya Chauta. Hanayo ankavutika kwambiri mumtima mwake, ndipo adapemphera kwa Chauta, akulira ndi mtima woŵaŵa. Adalumbira kuti, “Inu Chauta Wamphamvuzonse, muyang'ane kuzunzika kwanga ndipo muyankhe pemphero langa, osandiiŵala ine mdzakazi wanu. Ndithu mukandipatsa mwana wamwamuna, ine ndidzampereka mwanayo kwa Inu Chauta masiku onse a moyo wake, ndipo pamutu pake sipadzapita lumo.” Iyeyo akupemphera chotero pamaso pa Chauta, Eli ankamuyang'ana pakamwa. Hana ankalankhula chamumtima, milomo yake yokha ndiyo inkagwedezeka, koma mau ake sankamveka. Nchifukwa chake Eli adamuyesa woledzera. Tsono adamufunsa kuti, “Mai, kodi mukhala chiledzerere mpaka liti? Pitani, akayambe watha vinyo mwamwayu.” Koma Hana adayankha kuti, “Iyai mbuyanga, sindidamwe vinyo kapena chakumwa chaukali chilichonse. Munthune ndili ndi chisoni choopsa. Ndakhala ndikulira kwa Chauta chifukwa cha chisoni changachi. Musayese kuti ine mdzakazi wanu ndine mkazi wachabechabe, pakuti nthaŵi yonseyi ndakhala ndikuulula kwa Chauta nkhaŵa yanga yaikulu ndi zovuta zanga.” Apo Eli adamuyankha kuti, “Pitani ndi mtendere, Mulungu wa Israele akupatseni zimene mwampemphazo.” Tsono Hana adati, “Mundikomerebe mtima mdzakazi wanune.” Pompo mkaziyo adachoka nakadya, ndipo sadaonekenso wachisoni. M'maŵa mwake Elikana ndi banja lake adadzuka m'mamaŵa, ndipo atatha kupembedza Chauta, adabwerera kwao ku Rama. Elikana adakhala ndi mkazi wake Hana, ndipo Chauta adamkumbuka Hanayo. Motero Hana adaima, ndipo adabala mwana wamwamuna namutcha dzina loti Samuele, kunena kuti, “Ndidachita kumpempha kwa Chauta.” Tsono Elikana ndi banja lake lonse adapitanso kukatsira nsembe ya chaka ndi chaka kwa Chauta, ndi kukakwaniritsa lonjezo lake. Koma Hana sadapite nao chifukwa adaauza mwamuna wake kuti, “Malinga mwanayu akaleka kuyamwa, ndidzapita naye kuti ndikampereke kwa Chauta, ndipo adzakhala komweko moyo wake wonse.” Elikana mwamuna wake adamuuza kuti, “Uchite zimene zikukukomera, uyembekeze mpaka mwanayo ataleka kuyamwa. Kungoti Chauta achitedi monga momwe afunira.” Choncho mkaziyo adatsalira, namalera mwana wake uja mpaka atamletsa kuyamwa. Atamuletsa kuyamwa, adapita naye ku nyumba ya Chauta ku Silo. Adatenga ng'ombe yamphongo ya zaka zitatu, ufa wa makilogramu khumi, ndi thumba lachikopa la vinyo. Ngakhale mwanayo anali wamng'ono ndithu, adapita nayebe. Kumeneko adapha ng'ombe yamphongo ija ndipo mwanayo adampereka kwa Eli. Tsono Hana adati, “Inu mbuyanga, ndikunenetsa kuti ndithudi ine ndine mkazi uja amene ndidaaimirira pano pamaso panu, ndikupemphera kwa Chauta. Mwana uyu ndidachita kupempha, ndipo Chauta wandipatsa chopempha changacho. Nchifukwa chake ndampereka kwa Chauta. Moyo wake wonse mwanayu adzakhala wake wa Chauta.” Ndipo onsewo adapembedza Chauta kumeneko. Hana adapemphera nati, “Mtima wanga ukukondwa chifukwa cha zimene Chauta wandichitira, Ndikuyenda ndi mdidi chifukwa cha Chauta. Pakamwa panga pakula nkuseka adani anga monyodola. Ndakondwa kwambiri chifukwa mwandipulumutsa. “Palibe woyera wina wofanafana ndi Chauta, palibe wina koma Iye yekha. Palibe thanthwe lina lotchinjiriza lofanafana ndi Mulungu wathu. Anthu inu musalankhulenso modzitama, pakamwa panu pasatuluke zodzikuza. Pakuti Chauta ndi Mulungu wanzeru, ndiye amene amaweruza ntchito za anthu. Ankhondo amphamvu mauta ao athyoka, koma anthu ofooka avala dzilimbe. Anthu amene kale adaali okhuta, tsopano akusuma, koma amene kale adaali ndi njala, tsopano akukhuta. Chumba chabala ana asanu ndi aŵiri, koma wobereka ana ambiri watsala yekha. Chauta amadzetsa imfa ndipo amabwezeranso moyo, amatsitsira ku manda, ndipo amaŵatulutsakonso. Chauta amasaukitsa ndipo amalemeretsa, amatsitsa ndipo amakweza. Amakweza osauka kuŵachotsa pa fumbi, amachotsa anthu osoŵa pa dzala, amaŵakhazika pamodzi ndi akalonga, amaŵapatsa mpando waulemu. Nsanamira za dziko lapansi nzake za Chauta, adakhazika dziko lapansi pa nsanamirazo. “Anthu okhulupirika Iye adzatchinjiriza moyo wao, koma anthu oipa adzazimirira mu mdima, pakuti munthu sapambana ndi mphamvu zake. Chauta adzatswanya adani ake, adzaŵaopsa ndi bingu kuchokera kumwamba. Chauta adzaŵaweruza mpaka ku mathero a dziko lapansi. Koma adzalimbikitsa mfumu yake, adzakuza mphamvu za wodzozedwa wake.” Tsono Elikana adabwerera kwao ku Rama. Koma mnyamata uja Samuele adatsala, ndipo ankatumikira Chauta pamaso pa wansembe Eli. Tsono ana a Eli anali achabechabe, sankasamalako za Chauta. Sankasamalanso za khalidwe loyenera ansembe pakati pa anthu. Ankachita motere: pamene munthu wina ankapereka nsembe, nyama ilikuŵira pa moto, mtumiki wake wa wansembe ankabwera, atatenga chiforoko cha mano atatu. Ankachipisa mu mphika, ndipo zonse zimene chiforoko chija chinkajinya, wansembe ankatenga kuti zikhale zake. Aisraele onse amene ankafika ku Silo, ana a Eli ankaŵachita mokhamokhamo. Kuwonjezera apo, mafuta asanatenthedwe, mtumiki wa wansembe ankabwera ndi kuuza munthu wopereka nsembeyo kuti, “Patse nyama yoti ndikaotchere wansembe. Pakuti sadzalandira nyama yophika, koma yosaphika.” Ndipo munthuyo akanena kuti, “Apserezeretu mafutaŵa poyamba, pambuyo pake ndiye mutenge monga momwe mufunira,” mtumiki uja ankati, “Iyai, patsiretu tsopano pompano. Ngati sutero, ndichita kukulanda.” Motero tchimo la ana a Eli linali lalikulu pamaso pa Chauta, pakuti ankanyoza nsembe za Chauta. Samuele pa unyamata wake ankatumikira pamaso pa Chauta, atavala efodi yabafuta. Chaka chilichonse mai wake ankamsokera mkanjo, ndi kukampatsa pamene ankapita ndi mwamuna wake kukapereka nsembe ya chaka ndi chaka. Tsono Eli ankadalitsa Elikana ndi mkazi wake, ponena kuti, “Chauta akupatseni ana mwa mkazi ameneyu, chifukwa cha mwana amene iye adampereka kwa Chauta.” Atatero, iwowo ankabwerera kwao. Chauta adadalitsadi Hana, ndipo adabala ana aamuna atatu ndi ana aakazi aŵiri. Ndipo mnyamata uja Samuele ankakula akutumikira Chauta. Tsopano Eli adafika pokalamba kwambiri, ndipo ankamva zonse zimene ana ake aamuna ankachita Aisraele onse, ndiponso zoti anawo ankagona ndi akazi otumikira pa chipata cha chihema chamsonkhano. Tsono adafunsa ana akewo kuti, “Chifukwa chiyani mukuchita zinthu zotere? Ndilikumvatu kwa anthu zonse zoipa zimene mukuchita. Iyai ana anga, zimene ndilikumva anthu a Chauta akusimba nkumafalitsa, si zabwino ai. Munthu akachimwira munthu mnzake, mwina Mulungu adzampepesera munthuyo. Koma akachimwira Chauta, adzampepesera ndani?” Koma anawo sadamvere mau a bambo wao, chifukwa kunali kufuna kwa Chauta kuti anawo aphedwe. Monsemo mnyamata uja Samuele ankakulabe mu msinkhu, ndipo ankapeza kuyanja pamaso pa Chauta ndi anthu omwe. Tsiku lina munthu wa Mulungu adafika kwa Eli namuuza kuti, “Chauta akuti, ‘Suja ndidadziwulula kwa banja la kholo lako Aroni pamene anali akapolo a Farao ku Ejipito? Ndipo ndidamsankha pakati pa mafuko onse a Israele, kuti akhale wansembe wanga, ndipo kuti azipita ku guwa langa lansembe, azifukiza lubani, ndi kumavala efodi pamaso panga. Ndidalipatsa banja la bambo wako gawo la nsembe zanga zonse zopsereza zimene Aisraele amapereka. Nanga chifukwa chiyani ukunyoza nsembe zanga ndi zopereka zanga zimene ndidalamula? Kodi ukulemekeza ana ako kupambana Ine, pomadzinenepetsa nonsenu ndi zakudya zokoma kwambiri za pa nsembe zanga zimene anthu anga Aisraele amapereka? Paja Ine Chauta, Mulungu wa Israele, ndidaalonjeza kuti anthu a pa banja lako ndi a pa banja la atate ako, azidzanditumikira nthaŵi zonse. Koma tsopano ndikuti zimenezo zithe basi! Ndidzachitira ulemu anthu ondichitira ulemu, koma anthu ondinyoza, Inenso ndidzaŵanyoza. Ndithudi, masiku akudza pamene ndidzachotse anyamata onse a m'banja la atate ako, kotero kuti siidzapezekanso nkhalamba pabanja pako. Tsono pakati pa mavuto ako, udzayang'ana ndi maso ansanje zabwino zonse zimene ndidzapatsa Aisraele ena. Sipadzapezekadi nkhalamba pabanja pako nthaŵi zonse. Komabe pabanja pako ndidzasungapo mmodzi wodzanditumikira pa guwa langa, azidzangokuliritsa ndi kukumvetsa chisoni mumtima mwako. Koma ena onse a banja lako adzaphedwa ku nkhondo akali anyamata abiriŵiri. Zimene zidzaŵagwere ana ako aŵiriwo, Hofeni ndi Finehasi, zidzakhala chizindikiro kwa iwe. Aŵiri onsewo adzafa tsiku limodzi. Pambuyo pake ndidzasankha wansembe wokhulupirika amene adzachita zinthu pomvera zimene mtima wanga ufuna ndiponso potsata maganizo anga. Ndidzammangira banja lolimba, ndipo adzatumikira pamaso pa wodzozedwa wanga nthaŵi zonse. Apo aliyense amene adzatsale pabanja pako adzabwera kudzampempha iyeyo tindalama kapena kachakudya. Adzanena kuti, “Mundilole ndizithandizako ansembe, kuti ndipezeko kanthu kakudya.” ’ ” Mnyamata uja Samuele ankatumikira Chauta, ndipo Eli ankamuyang'anira. Masiku amenewo mau a Chauta sankamveka kaŵirikaŵiri, ndipo kuwona zinthu m'masomphenya sikunkachitikanso kaŵirikaŵiri. Tsiku lina Eli anali gone kumalo kwake. Maso ake adaali atayamba kupenya mwachimbuuzi, kotero kuti sankatha kupenya bwino. Samuelenso anali gone m'Nyumba ya Chauta kumene kunali Bokosi lachipangano la Chauta. Nthaŵiyo nkuti nyale ya Mulungu isanazime. Tsono Chauta adaitana kuti, “Samuele, Samuele!” Iye adayankha kuti, “Ŵaŵa!” Adathamangira kwa Eli nati, “Ndabwera, ndamva kuitana.” Koma Eli adati, “Sindidakuitane, kagone.” Motero Samuele adapita kukagona. Pambuyo pake Chauta adamuitananso kuti, “Samuele!” Pompo Samuele adadzuka napita kwa Eli nakamuuza kuti, “Ndabwera, ndamva ndithu kuitana.” Koma Eli adati, “Sindidakuitane mwana wanga, kagone.” Pamenepo nkuti Samuele asanadziŵe Chauta, ndipo mau a Chauta nkuti asanaululidwe kwa iyeyo. Chauta adamuitananso Samuele kachitatu. Pompo adadzukanso, napita kwa Eli, nakanena kuti, “Ndabwera, mwandiitana ndithu basi.” Pamenepo Eli adazindikira kuti Chauta ndiye amene ankaitana mnyamatayo. Tsono adauza Samuele kuti, “Pita, kagone. Akakuitananso, ukanene kuti, ‘Lankhulani, Inu Chauta, poti mtumiki wanune ndilikumva.’ ” Choncho Samuele adapita kukagona kumalo kwake. Chauta adabwera nadzaimirira pomwepo, ndipo adaitananso monga nthaŵi zina zija kuti, “Samuele, Samuele!” Samuele adayankha kuti, “Lankhulani, poti mtumiki wanune ndilikumva.” Tsono Chauta adauza Samuele kuti, “Tamvera, patsala pang'ono kuti ndichite chinthu mu Israele chimene chidzadabwitsa aliyense amene adzachimva. Tsiku limenelo ndidzachitadi zonse zimene ndidalankhula za Eli ndi banja lake, kuyambira pa chiyambi mpaka potsiriza. Ndikumdziŵitsa Eliyo kuti ndili pafupi kulanga banja lake mpaka muyaya, chifukwa cha zoipa zimene ana ake ankandichita. Eli ankazidziŵa zimenezo, koma osaŵaletsa. Nchifukwa chake ndikulumbira kuti mlandu wa banja la Eli sudzatha konse mpaka muyaya, ngakhale adzapereke nsembe kapena zopereka zina.” Samuele adagona mpaka m'maŵa. Atadzuka adatsekula zitseko za nyumba ya Chauta. Ankachita mantha kumuuza Eli zimene Chauta adaamuululirazo. Koma Eli adamuitana nati, “Samuele mwana wanga.” Samuele adati, “Ŵaŵa!” Apo Eli adafunsa kuti, “Kodi nchiyani chimene Mulungu wakuuza? Usandibisire. Mulungu akulange ndithu, ukandibisira kanthu kalikonse pa zonse zimene wakuuza.” Choncho Samuele adamuuza zonse osambisira kanthu kalikonse. Ndipo Eli adati, “Ameneyo ndi Chauta. Nachite zimene zikumkomera.” Monse Samuele ankakula, Chauta anali naye, motero zonse zimene Samueleyo ankanena zinkachitikadi. Ndipo Aisraele onse, kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba, adadziŵa kuti Chauta adamsankha Samuele kuti akhale mneneri. Chauta ankadziwululabe ku Silo. Kumeneko ankamveketsa mau ake kwa Samuele polankhula naye. Ndipo mau ake a Samuele ankafika kwa Aisraele onse. Tsiku lina Aisraele adatuluka kukamenyana nkhondo ndi Afilisti. Adamanga zithando zankhondo ku Ebenezeri, ndipo Afilisti adamanga zithando zao ku Afeki. Afilisti adandanda kuyang'ana Aisraele, ndipo adayamba kumenyana. Nkhondo itakula, Afilisti adagonjetsa Aisraele napha Aisraele 4,000 pomenyaniranapo. Pamene magulu ankhondo adafika ku zithando, atsogoleri a Aisraele adafunsa kuti, “Chifukwa chiyani Chauta walola kuti Afilisti atigonjetse? Tiyeni tikatenge Bokosi lachipangano la Chauta ku Silo, kuti Chautayo abwere pakati pathu ndipo atipulumutse kwa adani athu.” Choncho adatuma anthu ku Silo kukatenga Bokosi lachipangano la Chauta Wamphamvuzonse wokhala pa akerubi. Ana aŵiri a Eli, Hofeni ndi Finehasi, adapita nao pamodzi ndi Bokosi lachipanganolo ku zithando zankhondo zija. Pamene Bokosi lachipangano la Chauta lidafika kuzithandoko, Aisraele onse adayamba kufuula kwambiri, kotero kuti nthaka idagwedezeka. Afilisti atamva phokoso la kufuulako adati, “Kodi kufuula kwakukulu kotere ku zithando za Ahebriku nkwa chiyani?” Atamva kuti Bokosi lachipangano la Chauta lafika kuzithandoko, Afilistiwo adachita mantha poti ankati, “Kwafika milungu kumeneko.” Ndipo adati, “Tsoka ife! Chinthu choterechi sichidachitikepo nkale lonse. Tili m'mavuto! Angathe ndani kutipulumutsa kwa milungu yamphamvuyi? Imeneyitu ndi milungu ija idapha Aejipito ndi miliri ya mtundu uliwonse m'chipululu muja. Limbani mtima, chitani chamuna, inu Afilisti, kuwopa kuti mungakhale akapolo a Ahebri, monga momwe iwowo analiri akapolo anu. Chitani chamuna, menyani nkhondo.” Motero Afilisti adamenya nkhondo ndipo Aisraele adagonjetsedwa kotheratu, nathaŵira kwao. Nthaŵiyo kudaphedwa Aisraele okwanira 30,000, ankhondo oyenda pansi. Ndipo Bokosi lachipangano la Chauta lidalandidwa. Ana aŵiri aja a Eli, Hofeni ndi Finehasi, nawonso adaphedwa. Munthu wina wa fuko la Benjamini adathaŵa kunkhondoko nakafika ku Silo tsiku lomwelo. Anali atang'amba zovala zake ndi kudzithira dothi kumutu, kuwonetsa chisoni. Atafika, adapeza Eli atakhala pa mpando pambali pa mseu akungoyang'ana, poti ankadera nkhaŵa Bokosi lachipangano la Chauta lija. Pamene Mbenjamini uja adaloŵa mumzindamo, nayamba kusimba zimene zidaachitika kunkhondoko, anthu onse amumzinda adalira kwambiri. Eli atamva kulirako, adafunsa kuti, “Kodi kulira kumeneku ndiye kuti kwachitika chiyani?” Tsono munthu uja adapita msanga kwa Eli, nayamba kumufotokozera. Nthaŵiyo nkuti Eli ali nkhalamba ya zaka 98, maso ake atachita khungu, kotero kuti sankathanso kupenya. Munthuyo adauza Eli kuti, “Ine ndine amene ndachoka ku nkhondo. Ndathaŵa kumeneko lero lomwe.” Eli adamufunsa kuti, “Nanga nkhondo yayenda bwanji, mwana wanga?” Iye adayankha kuti, “Aisraele athaŵa Afilisti ndipo anthu ophedwa pakati pathu ngambirimbiri. Ana anu onse aŵiri aja, Hofeni ndi Finehasi, aphedwa, nalonso Bokosi lachipangano la Chauta lalandidwa.” Pamene adangotchula za Bokosi lachipangano la Chauta, Eli adagwa chankhongo, kuchoka pa mpando wake pafupi ndi chipata. Adathyoka khosi naafa, poti adaali wokalamba ndiponso wonenepa kwambiri. Anali atatsogolera Aisraele zaka makumi anai. Nthaŵiyo mpongozi wa Eli, mkazi wa Finehasi anali ndi pathupi ndipo anali pafupi kuchira. Pamene adamva zakuti Bokosi lachipangano la Chauta lidalandidwa, ndiponso kuti Eli, mpongozi wake, pamodzi ndi mwamuna wake adafa, zoŵaŵa za pobala mwana zidamfikira mwadzidzidzi, mwana nkumabadwa. Popeza kuti mkaziyo anali pafupi kufa, akazi omuthandiza adamuuza kuti, “Limba mtima, wabala mwana wamwamuna.” Koma iye sadayankhe ngakhale kusamalako ai. Tsono mwanayo adamutchula dzina loti Ikabodi, ndiye kuti, “Ulemerero wachoka kwa Aisraele!” Adatero chifukwa chakuti Bokosi lachipangano la Mulungu linali litalandidwa, ndiponso chifukwa cha imfa ya Eli mpongozi wake ndi ya mwamuna wake. Mau ake anali omwewo akuti, “Ulemerero wachoka kwa Aisraele poti Bokosi lachipangano la Chauta lalandidwa.” Afilisti atalanda Bokosi lachipangano lija, adalinyamula kuchoka nalo ku Ebenezeri nakafika nalo ku Asidodi. Tsono adatenga Bokosilo nakaliika m'nyumba ya Dagoni, mulungu wao, pambali pa Dagoniyo. M'maŵa mwake anthu a ku Asidodi atadzuka m'mamaŵa, adangoona Dagoni atagwa chafufumimba patsogolo pa Bokosi lachipanganolo. Apo anthuwo adatenga fanolo, naliikanso pamalo pake. Koma m'maŵa mwakenso atadzuka, adangoonanso Dagoni uja atagwa, ali chafufumimba, patsogolo pa Bokosi lachipanganolo. Mutu wa Dagoni ndi manja ake omwe zinali zitaduka ndi kugwera pa chiwundo. Thunthu lake lokha la Dagoniyo ndilo limene lidamutsalira. Chimenechi ndicho chifukwa chake chimene ansembe a Dagoni ndi anthu onse amene amaloŵa m'nyumba ya Dagoni, sapondera pa chiwundo cha nyumbayo ku Asidodi, mpaka pano. Kenaka Chauta adalanga koopsa anthu a ku Asidodi. Iwowo pamodzi ndi anthu a m'dziko lozungulira adaŵalanga ndi mafundo. Anthuwo ataona m'mene zinthu zinaliri, adati, “Bokosi lachipangano la Mulungu wa Aisraele lisakhale ndi ife, pakuti Mulungu wao watilanga kwambiri ifeyo ndi mulungu wathu yemwe Dagoni.” Choncho adaitana akalonga onse a Afilisti kuti asonkhane, nafunsana kuti, “Tichite nalo chiyani Bokosi lachipangano la Chauta wa Aisraele?” Anthuwo adayankha kuti, “Bokosi limeneli litumizidwe ku Gati.” Motero adatumiza Bokosi lachipanganolo kumeneko. Koma atafika nalo ku Gati, Chauta adauvuta mzindawo, ndipo anthu adachita mantha kwambiri. Choncho anthu amumzindamo adazunzika kwabasi, ana ndi akulu omwe, kotero kuti mafundo ankaŵatuluka anthu onsewo. Tsono adatumiza Bokosi lachipanganolo ku Ekeroni. Koma litangofika ku Ekeroniko, anthu akumeneko adalira kuti, “Bokosi lachipangano la Mulungu wa Aisraele, abwera nalo kwathu kuno, kuti atiphetse ife pamodzi ndi anthu athu.” Nchifukwa chake adaitananso akalonga onse a Afilisti kuti asonkhane, ndipo adati, “Chotsani Bokosili, ndipo mulibwezere kumene lidachokera, kuti lingatiphe ife pamodzi ndi anthu athu.” Pakuti munali mantha aakulu zedi mumzinda monsemo. Mulungu ankaŵalanga koopsa anthu akumeneko. Anthu amene sadafe, adavutika ndi mafundo, ndipo kulira kwa anthu amumzindamo kudamveka mpaka kumwamba. Bokosi lachipangano la Chauta lidakhala m'dziko la Afilisti miyezi isanu ndi iŵiri. Tsono Afilisti adaitana ansembe ao ndi anthu amaula naŵafunsa kuti, “Tichite nalo chiyani Bokosi lachipanganoli? Tiwuzeni. Kodi Bokosi limeneli tingalibwezere ku malo ake mwa njira yanji?” Iwo adati, “Mukafuna kubwezera Bokosili, musalitumize lopanda kanthu, koma mwa njira iliyonse mulitumize pamodzi ndi mphatso, kuti ikhale nsembe yopepesera machimo. Pambuyo pake mudzachira, ndipo pamenepo mudzadziŵa chifukwa chiyani chilango cha Mulungu sichikukuchokani.” Apo anthuwo adafunsa kuti, “Kodi nsembe yopepesera machimoyo idzakhale ya mtundu wanji?” Iwo adayankha kuti, “Idzakhale zifanizo zagolide za mafundo asanu ndi za mbeŵa zisanu kuŵerengetsa akalonga asanu a Afilisti, pakuti mliri womwewo unali pa inu nonse ndi pa akalonga anu. Tsono mupange zifanizo za mafundo anu aja ndi za mbeŵa zimene zikuwononga m'dziko mwanu, ndipo mulemekeze Mulungu wa Aisraele. Mwina mwake sadzakuvutaninso, inu ndi milungu yanu ndi dziko lanu. Chifukwa chiyani mukufuna kukhala okanika ngati Aejipito aja ndi Farao? Kodi Aejipitowo, Mulungu ataŵazunza, suja adaŵalola Aisraele kuti apite, ndipo adapitadi? Ndiye inu, konzani galeta latsopano ndipo mutenge ng'ombe ziŵiri zazikazi zamkaka zimene sizidavalepo goli ndi kale lonse. Mumange ng'ombezo ku galeta, koma makonyani ake muŵasiye kumudzi kwanu. Tsono mutenge Bokosi lachipanganolo, muliike pa galeta, ndipo pambali pake muikepo bokosi la zinthu zagolide zija zimene mukutumiza kwa Chauta, kuti zikhale nsembe yopepesera machimo. Pambuyo pake muzitaye ng'ombezo ndipo galeta lizipita. Tsono muziliyang'ana. Likamangopita kulondola kwao kwa Bokosilo mpaka kukafika ku Betesemesi, ndiye kutidi ndi Mulungu wa Aisraele amene adatidzetsera zovuta zazikuluzi. Koma zikapanda kutero, tidzadziŵa kuti sindiye amene adatizunza, zidangochitika mwatsoka.” Anthu aja adachitadi momwemo. Adatenga ng'ombe ziŵiri zamkaka nazimanga ku galeta, natsekera makonyani ake m'khola. Ndipo adaika Bokosi lachipangano pa galeta, ndi bokosi lija m'mene munali mbeŵa zagolide ndi zifanizo za mafundo ao. Tsono ng'ombezo zidapita molunjika potsata mseu waukulu wokafika ku Betesemesi, zikunka zikulira. Sizidacheukire kumanzere kapena kumanja, ndipo akalonga a Afilisti ankazitsata pambuyo, mpaka kukafika ku malire a ku Betesemesi. Nthaŵiyo anthu a ku Betesemesi ankadula tirigu m'chigwa. Ndipo pamene adati tha, napenya Bokosi lachipanganolo likubwera, adakondwa. Galeta lija lidafikira ku munda wa Yoswa ku Betesemesi ndi kuima komweko. Kumeneko kunali mwala waukulu. Tsono anthu am'mudzimo adaliŵaza nkhuni galetalo ndipo adapha ng'ombezo nazipereka kwa Chauta ngati nsembe yopsereza. Alevi anali atatsitsa Bokosi lachipangano la Chauta ndi bokosi lina lija la pambali pake m'mene munali zinthu zagolide, naŵaika pa mwala waukuluwo. Ndipo anthu a ku Betesemesi adapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zina kwa Chauta pa tsiku limenelo. Akalonga asanu a Afilisti aja ataona zimenezo, adabwerera ku Ekeroni tsiku lomwelo. Zifanizo zagolide za mafundo zija zimene Afilisti adapereka ngati nsembe zopepesera Chauta, zinkakhalira mizinda isanu: chimodzi chinali cha ku Asidodi, china cha ku Gaza, china cha ku Asikeloni, china cha ku Gati, china cha ku Ekeroni. Nazonso zifanizo zagolide za mbeŵa adazipereka moŵerengetsa mizinda yonse ya Afilisti imene inali ya akalonga asanu aja. Ina inali mizinda yamalinga, ina inali midzi yapamtetete. Mwala waukulu uja umene adaikapo Bokosi lachipangano lija m'munda wa Yoswa ku Betesemesi, udakalipo mpaka pano ngati mboni. Pambuyo pake Chauta adaphapo anthu 70 a ku Betesemesi chifukwa choti adaasuzumira m'Bokosi lachipangano, ndipo anzao adalira, popeza kuti Chauta adaapha anthu ambiri pakati pao. Tsono anthu a ku Betesemesi adati, “Angathe ndani kuima pamaso pa Chauta, Mulungu woyerayu? Ndipo Bokosi lachipanganoli lidzapita kuti likachoka kuno?” Choncho adatuma amithenga kwa nzika za ku Kiriyati-Yearimu kukanena kuti, “Afilisti abweza Bokosi lachipangano la Chauta. Bwerani kuno, mudzalitenge, kupita nalo kwanuko.” Anthu a ku Kiriyati-Yearimu adadzatenga Bokosi lachipanganolo nakafika nalo ku nyumba ya Abinadabu pa phiri. Ndipo adasankha mwana wake, Eleazara, kuti akhale woyang'anira Bokosilo. Kuyambira tsiku limene Bokosi lachipangano lija lidakhala ku Kiriyati-Yearimu, padapita nthaŵi yaitali ya zaka makumi aŵiri. Ndipo Aisraele onse adadandaulira Chauta kuti aŵathandize. Pamenepo Samuele adauza mtundu wonse wa Aisraele kuti, “Ngati mukubwerera kwa Chauta ndi mtima wanu wonse, muchotse milungu yachilendo ndi Aasitaroti pakati panu, mtima wanu ukhale pa Chauta ndi kutumikira Iye yekha. Mukatero adzakupulumutsani kwa Afilisti.” Choncho Aisraele adachotsa Abaala ndi Aasitaroti, nayamba kutumikira Chauta yekha. Tsono Samuele adati, “Sonkhanitsani mtundu wonse wa Aisraele ku Mizipa, ndipo ine ndikupemphererani kwa Chauta.” Choncho adasonkhana ku Mizipa, natunga madzi ndi kuŵathira pansi pamaso pa Chauta mopepesera, ndipo adasala chakudya tsiku limenelo, namanena kuti, “Tidachimwira Chauta.” Nku Mizipako kumene Samuele ankaweruza milandu ya Aisraele. Afilisti atamva kuti Aisraele adasonkhana ku Mizipa, akalonga a Afilisti adapita kuti akachite nawo nkhondo. Aisraele atamva zimenezi, adachita nawo mantha Afilistiwo, ndipo adauza Samuele kuti, “Musaleke kutidandaulira kwa Chauta, Mulungu wathu, kuti atipulumutse kwa Afilistiŵa.” Choncho Samuele adatenga mwanawankhosa woyamwa, nampereka wathunthu ngati nsembe yopsereza kwa Chauta. Adapempherera Aisraele kwa Chauta, ndipo Chauta adamuyankha. Pamene Samuele ankapereka nsembe yopsereza ija, Afilisti adasendera pafupi kuti amenyane ndi Aisraele. Koma Chauta adaŵaopsa Afilistiwo ndi mau onga bingu, naŵasokoneza, mwakuti adamwazikana pamaso pa Aisraele. Tsono Aisraele adatuluka ku Mizipa naŵalondola Afilistiwo, mpaka kubzola Betekara, akuŵapha njira yonse. Pambuyo pake Samuele adatenga mwala, nauimiritsa pakati pa Mizipa ndi Sene, ndipo adautcha dzina loti Ebenezeri, ndiye kuti “Mwala wachithandizo,” pakuti adati, “Mpaka pano Chauta wakhala akutithandiza.” Choncho Afilisti adagonjetsedwa, ndipo sadaloŵenso m'dziko la Aisraele. Chauta ndiye ankalimbana ndi Afilisti nthaŵi yonse Samuele ali moyo. Mizinda imene Afilisti anali atalanda idabwezedwanso kwa Aisraele, kuchokera ku Ekeroni mpaka ku Gati. Motero Aisraele adapulumutsa dziko lao kwa Afilisti. Panalinso mtendere pakati pa Aisraele ndi Aamori. Samuele adatsogolera Aisraele moyo wake wonse. Chaka ndi chaka ankapanga ulendo wozungulira, kupita ku Betele, Giligala ndi ku Mizipa, ndipo ankaweruza milandu ku malo onseŵa. Pambuyo pake ankabwerera ku Rama, poti ndiko kunali kwao. Kumenekonso ankaweruza Aisraele, ndipo adamangirako Chauta guwa. Samuele atakalamba, adaika ana ake kuti akhale oweruza Aisraele. Mwana wake wachisamba anali Yowele, wachiŵiri anali Abiya. Iwoŵa ankaweruza ku Beereseba. Koma ana akewo sanali ndi makhalidwe abwino a bambo wao, ankapotokera ku zoipa, namatsata phindu. Ankalandira ziphuphu, namaweruza milandu mopanda chilungamo. Tsono akuluakulu onse a Aisraele adasonkhana nadza kwa Samuele ku Rama. Adamuuza kuti, “Taonani, inu tsopanotu mwakhwima, ndipo ana anu sali ndi makhalidwe onga anu. Tsono mutipatse mfumu kuti izitilamulira, monga m'mene ikuchitira mitundu ina ya anthu.” Mau ameneŵa akuti “Mutipatse mfumu yoti izitilamulira” sadamkondwetse Samuele. Nchifukwa chake Samueleyo adapemphera kwa Chauta. Apo Chauta adayankha kuti, “Umvere zonse zimene anthuwo akukuuza. Sakukana iwe koma Ine. Sakufuna kuti ndikhale mfumu yao. Kuyambira tsiku limene ndidaŵatulutsa ku Ejipito mpaka pano, zochita zao nzokhazokha za kundikana ine ndi kutumikira milungu ina. Tsono nawenso akukuchita zomwezo. Motero tsono umvere zimene iwowo akunena. Koma ndiye uŵachenjeze kwambiri, ndipo uŵauzitse za mkhalidwe wake wa mfumu imene izidzaŵalamulirayo.” Choncho Samuele adaŵauza anthu amene ankafuna mfumu aja mau onse a Chauta. Adati, “Izi ndizo zimene mfumu yanuyo izidzakuchitani: izidzakulandani ana anu aamuna kuti akhale ankhondo, ena pa magaleta ake ankhondo, ena pa akavalo ake, ndipo ena othamanga patsogolo pa magaletawo. Ena idzaŵaika kuti akhale olamulira ankhondo chikwi chimodzi kapena makumi asanu. Ndipo ena azidzalima kumunda kwake ndi kumakolola zolima zake, kusula zida zankhondo ndiponso zipangizo za magaleta ankhondo. Izidzatenga ana anu aakazi kuti azidzayenga mafuta onunkhira, ndi kumaphika chakudya ndi kumapanga buledi. Idzakulandani minda yanu yabwino kwambiri, minda yanu yamphesa ndi yaolivi, kudzanso minda yanu yazipatso, ndi kuipatsa nduna zake. Idzalanda gawo lachikhumi la tirigu wanu ndi la mphesa zanu, nidzapatsa kwa akapitao ake ndi nduna zake. Idzakulandani antchito anu aamuna ndi adzakazi anu. Idzakulandaninso ng'ombe zanu zonenepa ndi abulu anu, ndi kumazigwiritsa ntchito zake. Idzalanda chigawo chachikhumi cha nkhosa zanu, ndipo inuyo mudzakhala akapolo ake. Nthaŵi imeneyo ikadzafika, mudzalira komvetsa chisoni chifukwa cha mfumu imene mwadzisankhirayo, koma Chauta sadzakuyankhani.” Koma anthuwo adakana kumvera mau a Samuele. Adati, “Iyai! Ife tikufuna mfumu yotilamulira. Tikufuna kuti nafenso tikhale ngati mitundu ina yonse, ndipo kuti mfumu yathu izitiweruza, kutitsogolera ndi kumatimenyera nkhondo.” Samuele atamva mau onse a anthuwo, adakakambira Chauta mau onsewo. Tsono Chauta adauza Samuele kuti, “Umvere zimene akunena, ndipo uŵapatse mfumu.” Choncho Samuele adauza Aisraelewo kuti, “Nonse bwererani kwanu.” Panali munthu wina wotchuka, wa ku dera la Benjamini, dzina lake Kisi, mwana wa Abiyele, mwana wa Zerori, mwana wa Bekorati, mwana wa Afiya, wa fuko la Benjamini. Iyeyo anali ndi mwana dzina lake Saulo, mnyamata wokongola. Pakati pa Aisraele onse panalibenso mnyamata wokongola kupambana iyeyo. Anali wamtali kotero kuti anthu ena onse ankamugwa m'mapewa. Tsiku lina Kisi adaona kuti abulu ake asoŵa. Choncho adauza Saulo kuti, “Tenga mmodzi mwa anyamata antchitoŵa, munyamuke, mukaŵafunefune abuluwo.” Iwo adabzola dziko lamapiri la Efuremu ndi la Salisa, koma osaŵapeza. Kenaka adabzola dziko la Salimu, koma kumeneko kunalibenso. Adabzolanso dziko la Benjamini, koma osaŵapezabe. Atafika ku dziko la Zufu, Saulo adauza mnyamata wake amene anali naye kuti, “Tiye tizibwerera, kuwopa kuti bambo wanga angaleke kusamala za abulu ndi kudera nkhaŵa za ife.” Koma mnyamatayo adati, “Mumzindamu muli munthu wa Mulungu, munthu amene onse amamchitira ulemu. Zonse zimene amanena zimachitikadi. Bwanji tipite kumeneko. Mwina mwake angathe kutiwuza za ulendo wathuwu.” Saulo adafunsa mnyamata wakeyo kuti, “Tsono tikapita, timtengere chiyani munthuyo? Buledi amene adaali m'matumba mwathu watha, ndipo tilibe ndi mphatso yomwe yoti tingampatse munthu wa Mulunguyo. Kodi tili ndi chiyani?” Mnyamatayo adayankha kuti, “Pano ndili ndi kandalama kakang'ono kasiliva, ndipo ndikapereka kwa munthu wa Mulunguyo, kuti atiwuze kumene kwapita abuluwo.” (Kale ku Israele, munthu akamapita kukapempha nzeru kwa Mulungu, ankati, “Tiyeni tipite kwa mlosi.” Ndiye kuti munthu amene tsopano amamutchula mneneri, kale ankatchulidwa mlosi). Tsono Saulo adauza mnyamata wakeyo kuti, “Chabwino. Tiye tizipita.” Choncho adapita kumzinda kumene kunali munthu wa Mulunguko. Pamene ankakwera phiri kupita kumzindako, adakumana ndi atsikana akutuluka mumzindamo kukatunga madzi, ndipo adaŵafunsa kuti, “Kodi mlosi uja alipo?” Iwo adayankha kuti, “Inde, alipo. Akunka patsogolo panupa. Fulumirani. Wangofika tsopano apa mumzindamu, chifukwa anthu akukapereka nsembe lero ku kachisi ku phiri. Mukangoloŵa mumzindamo, mumpeza asanapite kukachisiko kuti akadye. Anthu sangayambe kudya mpaka iye atabwera, poti ayenera kuyamba waidalitsa nsembeyo. Pambuyo pake ndiye anthu oitanidwa adzayamba kudya. Tsono pitani, mukumana naye posachedwa.” Choncho adapita kumzindako. Poloŵa mumzindamo, adaona Samuele akutuluka kumene, alikudza kwa iwo pa njira yopita kukachisi kuja. Koma chadzulo, Saulo asanabwere, nkuti Chauta atamdziŵitsiratu Samuele kuti, “Maŵa nthaŵi yonga yomwe ino, ndidzakutumizira munthu wa ku dera la Benjamini, udzamudzoze kuti akhale mfumu ya anthu anga Aisraele. Adzapulumutsa anthu kwa Afilisti. Ndaona kuzunzika kwao, ndipo ndamva kulira kwao.” Samuele ataona Saulo, Chauta adamuuza kuti, “Ndi ameneyu munthu ndidakuuza uja. Ndiye amene adzalamulire anthu anga.” Tsono Saulo adayandikira Samueleyo ku chipata namufunsa kuti, “Zikomo, kodi kunyumba kwa mlosi nkuti?” Samuele adamuyankha kuti, “Mlosiyo ndine. Tsogolaniko ku kachisi, poti lero mudya nane, ndipo m'maŵa ndikuuzani zonse zimene zili mumtima mwanu, kenaka ndidzakulolani kuti mupite. Musadandaule za abulu anu amene akhala akusoŵa masiku atatu apitaŵa, poti adapezeka kale. Kodi ndani amene Aisraele akumfunitsitsa? Kodi sindiwe ndi banja lonse la bambo wako?” Saulo adayankha kuti, “Komatu ine ndine Mbenjamini, fuko laling'ono pakati pa mafuko onse a Aisraele. Kodi banja langa sindiye laling'ono kwambiri pakati pa mabanja a fuko la Benjamini? Chifukwa chiyani mukundilankhula zotere?” Tsono Samuele adatenga Saulo ndi mnyamata wake uja, ndipo adaloŵa nawo m'chipinda chachikulu, naŵapatsa malo kutsogolo kwa anthu oitanidwa, amene onse pamodzi anali ngati anthu makumi atatu. Adauza wophika kuti, “Bwera nayo nthuli yanyama ija ndidaakupatsayi. Paja ndidaakuuza kuti uiike pambali.” Choncho wophika uja adatenga mwendo wa nyama naupereka kwa Saulo. Ndipo Samuele adati, “Nayi nyama imene ndidaakusungira. Idya, chifukwa ndidaakuikira padera kuti pa nthaŵi yake ino, uidye pamodzi ndi anthu amene ndidaŵaitana.” Choncho Saulo adadya ndi Samuele tsiku limenelo. Ndipo pamene adatsika kuchokera kukachisi kuja kukaloŵa mu mzinda, adamukonzera Saulo pogona pamwamba pa denga, ndipo iye adagona pamenepo. Tsono mbandakucha Samuele adaitana Saulo padengapo kuti, “Dzuka, ndikuperekeze, ndikutule apo.” Pompo Saulo adadzuka, ndipo onse aŵiriwo adakaloŵa mu mseu. Atafika kothera kwake kwa mzindawo, Samuele adauza Saulo kuti, “Uza mnyamatayu kuti abatsogola, iwe wekha uime pang'ono, kuti ndikuuze mau ochokera kwa Mulungu.” Mnyamata uja adatsogola. Tsono Samuele adatenga nsupa ya mafuta nathira mafutawo pamutu pa Saulo. Ndipo adamumpsompsona nati, “Chauta akukudzoza kuti ukhale mfumu ya anthu ake Aisraele. Udzalamulira anthu a Chauta ndi kuŵapulumutsa kwa adani oŵazungulira. Chizindikiro chakuti Chauta wakudzoza kuti ukhale mfumu yolamulira anthu ake, ndi ichi: ukachoka pano lero, ukumana ndi anthu aŵiri ku manda a Rakele ku Zeliza m'dziko la Benjamini. Iwowo akuuza kuti abulu unkafuna aja adapezeka, ndiponso kuti bambo wako waleka kusamala za abuluwo, koma akudera nkhaŵa za iwe, akunena kuti, ‘Nditani ine m'mene mwana wanga sakuwonekamu?’ Tsono utabzola pamenepo, ufika pa mtengo wogudira wa ku Tabori. Kumeneko ukumana ndi anthu atatu, wina atanyamula anaambuzi atatu, wina atanyamula mitanda itatu ya buledi, ndipo wina atanyamula thumba lachikopa la vinyo, akupita kukapereka nsembe kwa Mulungu ku Betele. Atakupatsa moni, akuninkhako mitanda iŵiri ya buledi, iwe uilandire. Pambuyo pake mufika ku phiri la Mulungu ku Gibea kumene kuli gulu lankhondo la Afilisti. Ndipo kumeneko, pamene mukuyandikira mzindawo, mukumana ndi gulu la aneneri akutsika kuchokera ku kachisi ku phiri, akuimba zeze, ting'oma, chitoliro ndi pangwe, ndipo akulosa. Pamenepo mzimu wa Chauta ukuloŵa mwamphamvu, ndipo nawenso uyamba kulosa nao, usinthika ndi kukhala munthu wina. Tsono ukaona zizindikiro zimenezi, uchite chilichonse choyenera nthaŵi imeneyo, poti Mulungu ali nawe. Udzatsogola ndiwe kupita ku Giligala. Patapita masiku asanu ndi aŵiri, ndidzabwera kudzapereka nsembe zopsereza ndi zamtendere. Kumeneko ndidzakulangiza zoti uchite.” Pamene Saulo adatembenuka kuti asiyane ndi Samuele, mtima wake Mulungu adausandutsa winawina. Ndipo zizindikiro zonse zija zidachitikadi tsiku limenelo. Atafika ku Gibea, adakumana ndi gulu la aneneri. Tsono mzimu wa Mulungu udamloŵa Sauloyo mwamphamvu, nayamba kulosa nao. Onse amene ankamdziŵa kale, ataona kuti akulosa limodzi ndi aneneri, adayamba kufunsana kuti, “Chamchitikira nchiyani mwana wa Kisi? Kani Saulonso ali m'gulu la aneneri?” Munthu wina wakomweko adayankhako nati, “Nanga enaŵa ndiye abambo ao ndani?” Nchifukwa chake padayambika chisudzo chakuti, “Kani Saulonso ali m'gulu la aneneri?” Atatha kulosako, Saulo adapita ku kachisi ku phiri. Mbale wa bambo wake wa Saulo ataona Sauloyo ndi mnyamata uja, adaŵafunsa kuti, “Mudaapita kuti?” Saulo adayankha kuti, “Tidaakafunafuna abulu. Titaona kuti sakupezeka, tidaapita kwa Samuele.” Apo mbale wa bambo wakeyo adati, “Ndikukupempha, uzeko zimene adanena Samuele.” Saulo adati, “Samuele adatiwuza bwino lomwe kuti abuluwo adapezeka.” Koma sadanene kanthu za nkhani ya ufumu ija imene Samuele adaamuuza. Tsono Samuele adaitana anthu ku msonkhano wachipembedzo ku Mizipa. Adauza Aisraele onse kuti, “Chauta, Mulungu wa Aisraele, akuti, ‘Ndidakutulutsani inu Aisraele ku dziko la Ejipito, ndipo ndidakupulumutsani kwa Aejipito ndi kwa mafumu onse amene ankakusautsani.’ Koma lero lino, inu mwamkana Mulungu wanu amene amakupulumutsani m'mavuto anu onse ndi m'masautso anu. Mukuti, ‘Iyai! Koma mutipatse mfumu yotilamulira.’ Nchifukwa chake tsono musonkhane pamaso pa Chauta potsata mafuko anu ndi mabanja anu.” Choncho Samuele adasonkhanitsa mafuko onse a Aisraele, ndipo pochita maere, fuko la Benjamini ndilo lidasankhidwa. Adasonkhanitsa fuko la Benjamini banja ndi banja, ndipo pochita maere, banja la Matiri ndilo lidasankhidwa. Potsiriza pake adasonkhanitsa anthu a m'banja la Matiri mmodzimmodzi, ndipo pochita maere, Saulo mwana wa Kisi, ndiye adasankhidwa. Koma pamene adamfunafuna, sadampeze. Tsono anthuwo adafunsa Chauta kuti, “Mwati munthuyo wafika kuno?” Chauta adayankha kuti, “Inde, akubisala pakati pa katundu.” Choncho adathamanga kukamtenga kumeneko. Ndipo ataimirira pakati pa anthu, ankaoneka wamtali, mwakuti anthu ena onse ankamugwa m'mapewa. Tsono Samuele adafunsa anthu onsewo kuti, “Kodi mukumuwona munthu amene Chauta wamsankha? Palibe wina wonga ameneyu pakati pa anthu onse.” Ndipo anthu onse adafuula kuti, “Amfumu akhale ndi moyo wautali!” Tsono Samuele adafotokozera anthu zinthu zoyenera mfumu pa maudindo ake. Ndipo adazilemba m'buku nakaliika bukulo pa malo oyera pamaso pa Chauta. Pambuyo pake Samuele adauza anthu kuti abwerere kwao. Saulo nayenso adapita kwao ku Gibea, ndipo adatsakana naye anthu amphamvu amene Mulungu adaŵafeŵetsa mtima. Koma anthu ena achabechabe adati, “Kodi munthu ameneyu angathe bwanji kutipulumutsa ife?” Ndipo adayamba kumnyoza Sauloyo, osampatsa ndi mphatso zomwe. Koma iye adangokhala chete. Patapita ngati mwezi umodzi, Nahasi Mwamoni adanka ndi gulu lankhondo kukazinga mzinda wa Yabesi m'dziko la Giliyadi. Tsono anthu onse a mu mzinda wa Yabesi adapempha Nahasiyo kuti, “Muchite nafe chipangano, ndipo tidzakutumikirani.” Koma Nahasi adaŵauza kuti, “Ndidzachita nanu chipangano pokhapokha aliyense nditamkolowola diso la ku dzanja lamanja, kuti pakutero ndichititse manyazi Aisraele onse.” Akuluakulu a ku Yabesi adamuyankha kuti, “Mutiyembekeze masiku asanu ndi aŵiri, kuti titumize mithenga ku dziko lonse la Aisraele. Tsono ngati sipaoneka wina wotipulumutsa, pamenepo tidzadzipereka kwa inu.” Pamene amithenga adafika kwao kwa Saulo ku Gibea, nauza anthu nkhaniyo, onse adayamba kulira motaya mtima. Nthaŵi imeneyo nkuti Saulo akuchokera ku munda, akuyenda pambuyo pa ng'ombe zantchito. Tsono adafunsa kuti, “Chaŵavuta anthu nchiyani kuti azilira?” Pamenepo adamuuza nkhani ya anthu a ku Yabesi ija. Saulo atamva zimenezi, pomwepo mzimu wa Mulungu udamloŵa mwamphamvu, ndipo adapsa mtima kwabasi. Mwa ng'ombe zija adapatulapo ziŵiri nazipha, ndipo adazidula nthulinthuli. Kenaka adatuma amithenga aja kuti akapereke nthulizo ku dziko lonse la Israele, ndi kumakanena kuti, “Umu ndimo m'mene adzaichitira ng'ombe ya aliyense amene sadzatsata Saulo ndi Samuele.” Apo anthuwo adagwidwa ndi mantha oopa Chauta ndipo onse adanyamuka ndi mtima umodzi. Saulo adaŵasonkhanitsa ku Bezeki, naŵaŵerenga. Aisraele analipo 300,000, Ayuda analipo 30,000. Ndipo adauza amithenga a ku Yabesi aja kuti, “Mukaŵauze anthu akwanu kuti maŵa, dzuŵa likuwomba mtengo, adzapulumutsidwa.” Anthu a ku Yabesi atamva uthengawu, adasangalala zedi. Nchifukwa chake adauza Nahasi kuti, “Maŵa tidzadzipereka kwa inu, ndipo mutichite chilichonse chimene chikukomereni.” M'maŵa mwake, Saulo adagaŵa anthu ake m'magulu atatu. Ndipo adaloŵa pakati pa zithando zankhondo za Aamoni m'mamaŵa kusanache, napha Aamoniwo mpaka masana dzuŵa litatentha. Tsono amene adapulumuka adangoti balala, aliyense kwayekhakwayekha. Apo anthu adamufunsa Samuele kuti, “Ndani amene ankanena kuti, ‘Kodi Saulo nkutilamulira ife?’ Bwera nawoni anthuwo kuti tiŵaphe.” Koma Saulo adati, “Palibe munthu ndi mmodzi yemwe amene aphedwe lero lino, pakuti lero Chauta wagwira ntchito yopulumutsa Aisraele.” Tsono Samuele adauza anthuwo kuti, “Tiyeni tipite ku Giligala, tikatsimikizenso ufumu wa Saulo kumeneko.” Choncho Aisraele onse adapita ku Giligala ndipo kumeneko adalonga Sauloyo ufumu pamaso pa Chauta. Anthu adapereka nsembe zachiyanjano pamaso pa Chauta, ndipo Saulo pamodzi ndi Aisraele onse adasangalala zedi kumeneko. Pambuyo pake Samuele adauza Aisraele onse kuti, “Ndidamvera zonse zimene mudandiwuza, ndipo ndakupatsani mfumu kuti izikulamulirani. Tsopano mfumu ndiyo izikutsogolerani. Ine nkukalamba kuno, kumutuku imvi zati mbuu, ndipo ana anga muli nawo pamodzi. Ndakhala ndikukutsogolerani kuyambira ndili mnyamata mpaka pano. Ine ndili pompano, ngati chilipo chimene ndidalakwa, munditsutsiretu tsopano pamaso pa Chauta ndi pamaso pa wodzozedwa wake. Kodi ndani ndidamulandapo ng'ombe? Ndani ndidamulandapo bulu? Ndani ndidamdyererapo? Kodi ndani amene ndidamuzunza? Kodi nkwa yani ndidalandirapo chiphuphu choti nkundidetsa m'maso? Tsimikizeni, ndipo ndikubwezerani zonse.” Anthuwo adati, “Simudatidyerere, kapena kutizunza, ngakhale kutenga kanthu kalikonse ka munthu.” Apo Samuele adaŵauza kuti, “Chauta ndiye mboni pakati pa ine ndi inu, nayenso wodzozedwa wa Chauta ndiye mboni lero lino kuti simudandipeze chifukwa chilichonse.” Ndipo iwo adati, “Zoonadi, Chauta ndiye mboni.” Samuele adaŵauzanso kuti, “Chauta ndiye amene adasankha Mose ndi Aroni, kuti atulutse makolo anu m'dziko la Ejipito. Nchifukwa chake tsono imani pomwepa, kuti tikumbutsane pamaso pa Chauta za ntchito zonse zimene Iye adachita pokupulumutsani inu ndi makolo anu. Pamene Yakobe ndi banja lake adapita ku dziko la Ejipito, Aejipito namaŵazunza, pamenepo makolo anuwo adadandaula kwa Chauta. Ndipo Chauta adatuma Mose ndi Aroni kuti aŵatulutse ku Ejipito ndi kudzaŵakhazika ku malo ano. Koma makolo anuwo adaiŵala Chauta, Mulungu wao. Ndipo Mulungu adaŵapereka m'manja mwa Sisera, mtsogoleri wa ankhondo a mzinda wa Hazori. Adaŵaperekanso m'manja mwa Afilisti ndi m'manja mwa mfumu ya ku Mowabu. Adani onsewo adachita nkhondo ndi makolo anuwo. Tsono iwowo adadandaula kwa Chauta nati. ‘Ife tachimwa chifukwa choti tasiya Inu Chauta, ndipo tatumikira mafano aja a Baala ndi Asitaroti. Koma tsopano tipulumutseni kwa adani athu, ndipo tidzakutumikirani.’ Choncho Chauta adatuma Yerubaala, Balaki, Yefita ndi ine Samuele. Tidakupulumutsani kwa adani anu amene ankakuzingani, ndipo mudakhala pa mtendere. Tsono pamene mudaona kuti Nahasi, mfumu ya Aamoni, adadza kuti adzamenyane nane, mudandiwuza kuti, ‘Iyai, koma mfumu ndiyo imene idzatilamulire,’ chonsecho mfumu yanu inali Chauta, Mulungu wanu. “Tsopano nayi mfumu imene mudaisankha, imene mudachita kuipempha ija. Ndiyo imene Chauta wakupatsani. Mukamaopa Chauta ndi kumamtumikira ndi kumamvera mau ake, osakana malamulo ake, ndiponso ngati nonsenu pamodzi ndi mfumu yanu mudzatsata Chauta, Mulungu wanu, zonse zidzakuyenderani bwino. Koma mukapanda kumvera mau a Chauta nkumakana malamulo ake, ndiye kuti Iye adzakulangani inu ndi mfumu yanu yomwe. Nchifukwa chake tsono imani pomwepa, muwone chinthu chachikulu chimene Chauta akuchitireni mukupenya. Kodi ino si nthaŵi yachilimwe yodula tirigu? Komabe nditama Chauta mopemba kuti agwetse mvula yamabingu. Apo mudziŵa ndi kuwona kuti tchimo lanu limene mwachita popempha mfumu kwa Chauta nlalikulu.” Choncho Samuele adatama Chauta mopemba, ndipo Chauta adatumizadi mvula yamabingu tsiku limenelo. Motero anthu onse adagwidwa ndi mantha aakulu oopa Chauta ndi Samuele. Pamenepo anthu onse adauza Samuele kuti, “Chonde mutipempherere ife atumiki anu kwa Chauta, Mulungu wanu, kuti tingafe, pakuti pa machimo athu onse taonjezapo tchimo limeneli lopempha kuti tikhale ndi mfumu.” Samuele adaŵauza kuti, “Musaope. Kuchimwa mwachimwadi, komabe musaleke kutsata Chauta. Muzimtumikira ndi mtima wanu wonse. Ndipo musatsate mafano achabe amene alibe phindu, amene sangathe kupulumutsa poti ngopandapake. Chauta sadzataya anthu ake, kuti dzina lake lalikulu linganyozeke, poti chidamukondweretsa kuti akusandutseni anthu ake. Komanso kunena za ine, sindifuna kuchimwira Chauta, pakuleka kukupemphererani. Ndidzakuphunzitsani zimene zili zabwino ndi zolungama kuti muzizichita. Muzingoopa Chauta, ndipo muzimtumikira mokhulupirika ndi mtima wanu wonse. Nthaŵi zonse muziganizira zazikulu zimene wakhala akukuchitirani. Koma mukamachitabe zoipa, ndiye kuti inuyo pamodzi ndi mfumu yanu mudzaonongedwa.” Saulo adaloŵa ufumu ali ndi zaka 30, ndipo adalamulira Aisraele zaka ngati 42. Nthaŵi ina iye adasankha Aisraele 3,000. Mwa ameneŵa, 2,000 anali ndi Sauloyo ku Mikimasi ndi ku dziko lamapiri ku Betele, ndipo 1,000 anali ndi Yonatani ku Gibea m'dziko la Benjamini. Anthu ena onse otsala adaŵabweza kwao. Yonatani adapha mkulu wa ankhondo wachifilisti amene anali ku Geba, ndipo Afilisti adamva zimenezi. Apo Saulo adatuma amithenga kuti alize lipenga lankhondo m'dziko lonselo, nanena kuti, “Ahebri amve.” Ndipo Aisraele onse adamva mbiri yakuti Saulo adapha mkulu wa ankhondo wachifilisti, ndiponso kuti Afilisti anali ataipidwa kwambiri ndi Aisraele. Motero anthu adaitanidwa kuti abwere kwa Saulo ku Giligala. Tsono Afilisti adasonkhana pamodzi kuti amenyane nkhondo ndi Aisraele. Adasonkhanitsa magaleta ankhondo 30,000, okwera pa akavalo 6,000 ndi ankhondo ochuluka ngati mchenga wa m'mbali mwa nyanja. Iwowo adapita nakamanga zithando zao ku Mikimasi, kuvuma kwa Betaveni. Pamene Aisraele adaona kuti ali m'zoopsa, poti anali atapanikizidwadi kwambiri, adakabisala m'mapanga, m'maenje, m'matanthwe, m'makwaŵa ndi m'zitsime. Ena adaoloka Yordani mpaka kukafika ku dziko la Gadi ndi ku Giliyadi. Saulo anali ku Giligalabe, ndipo anthu okhala naye anali njenjenje ndi mantha. Sauloyo adadikira masiku asanu ndi aŵiri, monga momwe adaanenera Samuele. Koma Samueleyo sadafike ku Giligala, ndipo anthu adayamba kumthaŵira Saulo uja. Choncho Saulo adati, “Bwera nayoni kuno nsembe yopserezayo pamodzi ndi nsembe zachiyanjano zija.” Ndipo Saulo adapereka nsembe yopsereza ija. Atangomaliza kupereka nsembe yopserezayo, adangoona Samuele watulukira. Tsono Saulo adapita kukakumana naye ndi kumulonjera. Samuele adamufunsa Sauloyo kuti, “Nanga nchiyaninso mwachitachi?” Iye adayankha kuti, “Pamene ndinaona kuti anthu akundithaŵira, ndipo kuti inuyo nthaŵi imene mudaanena ija simudabwere, ndiponso kuti Afilisti adasonkhana ku Mikimasi, ndinati, ‘Tsopano Afilisti abwera kudzandithira nkhondo ku Giligala kuno, ine ndisanapemphe Chauta kuti andikomere mtima.’ Motero ndinadzikakamiza kupereka nsembe yopserezayi.” Apo Samuele adamuuza kuti, “Mwachitatu zopusa. Simudatsate zimene Chauta, Mulungu wanu, adakulamulani. Mukadazitsata, bwenzi Chauta atakhazikitsa ufumu wanu pakati pa Aisraele mpaka muyaya. Koma tsopano ufumu wanu sudzakhalitsa. Chauta wadzifunira yekha munthu wa kumtima kwake. Chauta wamsankha munthuyo kuti akhale mfumu yolamulira anthu ake, chifukwa inu simudatsate zimene Iye adakulamulani.” Atatero Samuele adanyamuka ku Giligala napita ku Gibea ku dziko la Benjamini. Saulo adaŵerenga anthu amene anali naye, ndipo adapeza kuti alipo 600. Tsono iyeyo ndi mwana wake Yonatani, pamodzi ndi anthu amene anali nawowo, adakhala ku Geba ku dziko la Benjamini. Koma Afilisti adamanga zithando zankhondo ku Mikimasi. Ankhondo a Filisti adatuluka kuchoka ku zithando zao m'magulu atatu. Gulu limodzi lidalunjika ku Ofura ku dziko la Suwala. Gulu lina lidalunjika ku Betehoroni, ndipo lina lidalunjika ku malire oyang'anana ndi chigwa cha Zeboimu chakuchipululu. Nthaŵi imeneyi nkuti mulibe msuli ndi mmodzi yemwe m'dziko lonse la Israele, chifukwa Afilisti ankati, “Tisaŵalole Ahebri kuti azidzisulira okha malupanga ndi mikondo.” Motero Mwisraele aliyense ankapita kwa Afilisti kukasanjitsa pulao kapena khasu lake, ndi kukanoletsa nkhwangwa yake kapena chikwakwa. Mtengo wonoletsera nkhwangwa unali ndalama imodzi, ndipo mtengo wosanjitsira makasu ndi wosongoletsera zisonga unali ndalama ziŵiri. Motero tsiku lankhondolo panalibe lupanga kapena mkondo m'manja mwa Mwisraele aliyense amene ankatsata Saulo ndi Yonatani. Koma Saulo ndi mwana wake Yonatani, iwo okha ndiwo anali nazo zida. Tsono Afilisti adatuma kagulu kankhondo kukalonda mpata wa Mikimasi. Tsiku lina Yonatani, mwana wa Saulo, adauza mnyamata womnyamulira zida zake zankhondo kuti, “Tiye tiwolokere tipite ku kaboma kankhondo ka Afilisti tsidya ilo.” Koma sadauze bambo wake. Saulo ankakhala m'malire a Gibea patsinde pa mtengo wa makangaza ku Migironi. Anthu amene anali naye analipo 600 pamodzi. Panalinso Ahiya, wansembe amene ankavala efodi. Iyeyo anali mwana wa Ahitubi, mbale wa Ikabodi mwana wa Finehasi. Finehasiyo anali mwana wa Eli, wansembe wa Chauta ku Silo. Tsono anthu sankadziŵa kuti Yonatani wachokapo. Pampata pamene Yonatani ankafuna kudzerapo kuti akafike ku kaboma kankhondo kaja, panali thanthwe lotsetsereka mbali ina, ndi lina lotsetsereka mbali inanso. Dzina la thanthwe lina ankati Bozezi, ndipo linalo ankati Sene. Thanthwe lina linali kumpoto kuyang'anana ndi Mikimasi, ndipo linalo linali kumwera kuyang'anana ndi Geba. Yonatani adauza mnyamata wake uja kuti, “Tiye tiwolokere tipite ku kaboma kankhondo ka anthu osaumbalidwaŵa. Mwina mwake Chauta atigwirira ntchito. Pakuti palibe chomletsa Chauta kutipambanitsa ngakhale tikhale ochepa chotani.” Mnyamata wakeyo adati, “Muchite zonse monga momwe mtima wanu ufunira. Ine ndili nanu, ndipo monga momwe mukuganizira inu, ine mmomwemonso.” Tsono Yonatani adati, “Tiwolokere kwa anthuwo, ndipo tikadziwonetse kwa iwo. Akatiwuza kuti, ‘Dikirani mpaka tikupezeni,’ tikangoima pamalo pathu, osapita kwa iwowo. Koma akanena kuti, ‘Bwerani kuno,’ ife tikapitadi, pakuti Chauta waapereka anthuwo m'manja mwathu. Chimenechi chidzakhala chizindikiro kwa ife.” Choncho aŵiriwo adadziwonetsa ku kaboma kankhondo ka Afilisti. Tsono Afilisti adati, “Taonani Ahebri akutuluka m'maenje m'mene ankabisala.” Ndipo anthu akukabomawo adafuulira Yonatani ndi mnyamata wake uja kuti, “Tabwerani kuno, muwona!” Apo Yonatani adauza mnyamata wakeyo kuti, “Unditsate, Chauta wapereka anthuŵa m'manja mwa Aisraele.” Choncho Yonatani adakwera chokwaŵa, mnyamata wake uja akumtsata pambuyo. Tsono Yonatani adaŵathira nkhondo Afilistiwo ndi kumaŵagwetsa, mnyamata wake uja nkumaŵapha pambuyo pa iyeyo. Anthu amene Yonatani ndi mnyamata wake uja adapha nthaŵi yoyamba analipo ngati makumi aŵiri, ndipo adaŵaphera pa malo ochepa okwanira ngati theka la ekala. Tsono Afilisti onse m'dzikomo adasokonezeka ndi mantha aakulu. Ankhondo a ku kaboma kankhondo kaja ndi anzao enanso ankanjenjemera kwambiri. Kudachita chivomezi ndipo kugwedezeka kwa dziko kudakulitsa mantha a Afilisti aja. Alonda a Saulo a ku Gibea ku dziko la Benjamini poti ayang'ane, adangoona chigulu cha adani chikumwazikira uku ndi uku. Tsono Saulo adauza anthu amene anali naye aja kuti, “Ŵerengani anthu, ndipo muwone amene achokapo.” Ataŵaŵerenga, adaona kuti Yonatani ndi mnyamata womnyamulira zida uja palibe. Apo Saulo adauza Ahiya kuti, “Bwera nayo kuno efodiyo.” Nthaŵi imeneyo efodiyo inali ndi Ahiya pamaso pa Aisraele. Pamene Saulo ankalankhula ndi wansembeyo, phokoso linkakulirakulira ku zithando za Afilisti. Tsono Saulo adauza wansembe uja kuti, “Leka, usaombeze!” Pamenepo Saulo pamodzi ndi anthu amene anali naye adasonkhananso napita kukamenya nkhondo, ndipo adaona Afilisti akungophana okhaokha. Motero kunali chisokonezo chachikulu kwambiri. Ahebri ena amene kale adaali pamodzi ndi Afilistiwo, ndipo anali atapita nao ku zithandozo, iwonso adatembenuka nakhala pamodzi ndi Aisraele a mbali ya Saulo ndi Yonatani. Chimodzimodzinso Aisraele amene adaabisala m'dziko lamapiri la Efuremu, atamva kuti Afilisti akuthaŵa, nawonso adaŵathamangira Afilistiwo naŵathira nkhondo. Ndipo nkhondoyo idapitirira mpaka kubzola mzinda wa Betaveni. Umu ndimo m'mene Chauta adapulumutsira Aisraele tsiku limenelo. Koma ankhondo a Aisraele adavutika tsiku limene lija, pakuti Saulo adaŵaopseza pakunena kuti, “Atembereredwe amene adye kanthu kusanade, ndisanalipsire adani anga.” Motero panalibe ndi mmodzi yemwe amene adalaŵa chakudya. Tsono onse adaloŵa m'nkhalango ina m'mene munali uchi. Ataloŵa m'nkhalangomo, adangoona uchi ukukha pansi, koma panalibe amene adatengako kuika pakamwa, poti ankaopa temberero lija. Koma Yonatani anali asanamve za temberero la bambo wake lija. Choncho adatosa chisa cha njuchi ndi nsonga ya ndodo imene inali m'manja mwake, naika uchi wake pakamwa naadya. Atatero m'maso mwake mudachita kuti ngwee. Tsono mmodzi mwa anthuwo adati, “Bambo wanu waopseza anthu pakunena kuti, ‘Atembereredwe amene adye kanthu lero.’ Nchifukwa chake anthuŵa akuchita ngati akomoke ndi njala.” Tsono Yonatani adati, “Bambo wanga wavutitsa anthu onse. Taonani ine m'maso mwanga mwayera, chifukwa ndalaŵako uchiwu. Kukadakhala bwino kwambiri, anthu akadadya mwaufulu lero zofunkha zimene adazipeza kwa adani ao. Zidakatero bwenzi tsopano lino titapha Afilisti ambiri.” Tsikulo Aisraele adapha Afilisti kuyambira ku Mikimasi mpaka ku Ayaloni. Koma Aisraelewo anali pafupi kukomoka nayo njala. Motero adathamangira pa zofunkha, ndipo adatenga nkhosa, ng'ombe ndi makonyani, nazipha. Ndipo adazidya pamodzi ndi magazi omwe. Koma ena adauza Saulo kuti, “Onani, anthu akuchimwira Chauta podyera kumodzi ndi magazi.” Saulo adati, “Mwaukira Chauta lero! Pezani mwala waukulu muukunkhunizire kuno.” Ndipo adatinso, “Mwazikanani pakati pa anthu, muŵauze kuti, ‘Aliyense abwere ndi ng'ombe yake, kapena nkhosa yake, aziphere pompano, kenaka adye. Ndipo musachimwire Chauta podyera kumodzi ndi magazi.’ ” Motero aliyense mwa anthuwo adabwera ndi ng'ombe yake usiku umenewo, naiphera komweko. Tsono Saulo adamangira Chauta guwa. Limeneli linali guwa loyamba limene Sauloyo adamangira Chauta. Pamenepo Saulo adati, “Tiyeni tipite usiku, tilondole Afilisti, ndipo tilande zinthu zao mpaka m'maŵa kutacha. Tisasiyepo ndi mmodzi yemwe mwa iwo.” Anthuwo adati, “Chitani chilichonse chimene chikukukomerani.” Koma wansembe adati, “Tiyeni tiyambe tapempha nzeru kwa Mulungu.” Tsono Saulo adafunsa Mulungu kuti, “Kodi tiŵalondole Afilistiŵa? Kodi muŵapereka m'manja mwathu?” Koma Mulungu sadamuyankhe kanthu tsiku limenelo. Apo Saulo adati, “Bwerani kuno nonse atsogoleri a anthu. Tiwone ndi tchimo lanji lachitika lero. Pali Chauta, Mpulumutsi wa Aisraele, wochimwayo ngakhale akhale mwana wanga Yonatani, afe ndithu.” Koma panalibe ndi mmodzi yemwe pakati pa anthu onsewo amene adamuyankha. Tsono adauza Aisraelewo kuti, “Inu mukhale mbali imodzi, ine ndi mwana wanga Yonatani tikhalanso mbali ina.” Anthuwo adauza Saulo kuti, “Muchite zimene zikukomereni.” Nchifukwa chake Saulo adati, “Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, chifukwa chiyani simudandiyankhe ine mtumiki wanu lero lino? Ngati wolakwa ndineyo kapena mwana wanga Yonatani, Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, aoneke ndi Urimu. Koma tchimolo likakhala la Aisraele, aoneke ndi Tumimu.” Maere adagwera Yonatani ndi Saulo, anthu nkupulumuka. Tsono Saulo adati, “Chitani maere pakati pa ine ndi mwana wanga Yonatani.” Ndipo maere adagwera Yonatani. Apo Saulo adauza Yonatani kuti, “Tandiwuza zimene wachita.” Yonatani adauza bambo wakeyo kuti, “Ndidalaŵako uchi pang'ono ndi nsonga ya ndodo yanga. Ndiye ai, chomwecho, ine ndili wokonzeka kuti ndife.” Apo Saulo adati, “Mulungu andilange ine, ngakhale kundipha kumene, ngati suufa iwe Yonatani.” Tsono anthu adafunsa Saulo kuti, “Kodi afe Yonatani amene wagwira ntchito yopulumutsa Aisraele kunkhondo? Sizingatheke mpang'ono pomwe. Pali Chauta wamoyo! Tsitsi nlimodzi lomwe la kumutu kwake silipezeka lothothoka. Zimene wachita lerozi, wamthandiza ndi Mulungu.” Motero anthu adamupulumutsa Yonatani, ndipo sadaphedwe. Pambuyo pake Saulo adaleka kuŵathamangira Afilisti, ndipo Afilistiwo adabwerera kwao. Pamene Saulo adakhala mfumu yolamulira Aisraele, adamenyana nkhondo ndi adani ake onse omzungulira. Adamenyana ndi Amowabu, Aamoni, Aedomu, mafumu a ku Zoba ndiponso Afilisti. Kulikonse kumene ankapita, ankaŵagonjetsa. Adachita zamphamvu, ndipo adagonjetsa Aamaleke. Motero adapulumutsa Aisraele kwa anthu amene ankaŵalanda zinthu zao. Ana aamuna a Saulo anali Yonatani, Isivi ndi Malikisuwa. Analinso ndi ana aŵiri aakazi, wamkulu anali Merabi, wamng'ono anali Mikala. Mkazi wa Saulo anali Ahinowamu mwana wa Ahimaazi. Ndipo mkulu wa ankhondo a Saulo anali Abinere, mwana wa Nere, mbale wa bambo wa Saulo. Kisi bambo wa Saulo ndipo Nere bambo wa Abinere, anali ana a Abiyele. Pa moyo wake wonse Saulo ankakhalira kuchita nkhondo ndi Afilisti. Tsono ankati akaona munthu wamphamvu kapena wolimba mtima, ankamulemba m'gulu lake lankhondo. Tsiku lina Samuele adauza Saulo kuti, “Paja Chauta adaatuma ine kuti ndikudzozeni, kuti mukhale mfumu ya anthu ake Aisraele. Nchifukwa chake tsono imvani uthenga wochokera kwa Chauta. Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, ‘Ndidzalanga Aamaleke chifukwa cha kumenyana ndi Aisraele pa njira, pamene Aisraelewo ankachokera ku Ejipito. Pitani tsono, mukaŵathire nkhondo Aamalekewo, mukaononge kwathunthu zinthu zao zonse. Musakasiyeko munthu ndi mmodzi yemwe, mukaphe amuna, akazi, ana ndi makanda omwe. Mukaphenso ng'ombe, nkhosa, ngamira ndi abulu onse.’ ” Choncho Saulo adaitana ankhondo ake, naŵaŵerenga ku Telaimu. Ankhondo oyenda pansi analipo 200,000, ankhondo a ku Yuda analipo 10,000 pamodzi. Ndipo Saulo adafika ku mzinda wa Aamaleke, naubisalira m'khwaŵa. Tsono adauza Akeni kuti, “Muchoke pakati pa Aamaleke, kuti ndingakuwonongereni kumodzi. Pakuti inu mudachitira chifundo Aisraele muja ankachokera ku Ejipitomu.” Motero Akeni adachoka pakati pa Aamaleke. Pamenepo Saulo adagonjetsa Aamaleke kuyambira ku Havila mpaka ku Suri, kuvuma kwa Ejipito. Adamtenga wamoyo Agagi, mfumu ya Aamaleke, ndipo adapha anthu ena onse ndi lupanga. Koma Saulo ndi anthu amene anali nawo, sadamuphe Agagi, sadaphenso nkhosa ndi ng'ombe zabwino koposa, anaang'ombe ndi anaankhosa onenepa, ndi zonse zimene zinkaoneka zabwino. Adangoononga zimene zinali zopanda ntchito ndi zachabechabe. Tsono Chauta adauza Samuele kuti, “Ndikumva chisoni kuti ndidampatsa ufumu Saulo. Wabwerera m'mbuyo, waleka kunditsata, ndipo sadamvere malamulo anga.” Pamenepo Samuele adapsa mtima, ndipo adadandaula kwa Chauta usiku wonse. M'mamaŵa ndithu, Samuele adadzuka kuti akakumane ndi Saulo. Anthu adamuuza kuti, “Saulo adabwera ku Karimele, ndipo kumeneko adadziimikira mwala wa chikumbutso cha iye mwini. Tsono adachokapo napitirira mpaka ku Giligala.” Samuele atafika kwa Saulo, Sauloyo adamuuza kuti, “Chauta akudalitseni. Ndachitadi zonse zimene Chauta adandilamula.” Koma Samuele adati, “Nanga bwanji ndikumva nkhosa ndi ng'ombe zikulira?” Saulo adayankha kuti, “Zimenezi adakazitenga kwa Aamaleke, pakuti anthu adasungako nkhosa ndi ng'ombe zabwino koposa, kuti akapereke nsembe kwa Chauta, Mulungu wanu. Koma zina zonse taziwononga kotheratu.” Apo Samuele adamuuza kuti, “Basi, musapitirize! Imani ndikukambireni zimene Chauta wandiwuza usiku.” Tsono Saulo adati, “Nenani.” Samuele adati, “Ngakhale kale munali wamng'ono pamaso pa anthu, tsopano mwasanduka mtsogoleri wa mafuko onse a Aisraele. Chauta adakudzozani kuti mukhale mfumu yomalamulira Aisraele. Ndipo Chauta adakutumani kuti, ‘Pita, ukaononge kwathunthu Aamaleke, anthu oipa mtima aja, ndipo uchite nawo nkhondo mpaka kuŵatheratu onsewo.’ Chifukwa chiyani nanga simudamvere mau a Chauta? Chifukwa chiyani mudathamangira zofunkha ndi kuchita zoipira Chauta?” Saulo adayankha kuti, “Iyai, inetu mau a Chauta ndidatsata, ndipo ndidapitadi kukachita zimene Chauta adandituma. Ndidagwira Agagi mfumu ya Aamaleke, ndipo ndidapha Aamaleke onse. Koma pa zofunkha anthu adatengako nkhosa ndi ng'ombe, ndi zina zabwino kwambiri, zimene zinkayenera kuwonongedwa, kuti akazipereke nsembe kwa Chauta, Mulungu wanu, ku Giligala.” Koma Samuele adati, “Kodi Chauta amakondwa ndi chiti: nsembe zopsereza ndi nsembe zina, kapena kumvera mau ake? Ndithu, ndi kumvera ndi kupereka nsembe kwabwino kwambiri nkumvera. Ndi kutchera khutu ndi kupereka mafuta ankhosa kwabwino kwambiri nkutchera khutu. Kugalukira kuli ngati tchimo loombeza, kukhala wokanika kuli ngati tchimo lopembedza mafano. Popeza kuti mwakana mau a Chauta, Iyenso wakukanani kuti musakhalenso mfumu.” Pamenepo Saulo adauza Samuele kuti, “Ndachimwa, ndalakwira lamulo la Chauta ndiponso malangizo anu, chifukwa chakuti ndinkaopa anthu ndipo ndinkamvera mau ao. Nchifukwa chake tsono pepani, ndagwira mwendo, mundikhululukire tchimo langa, ndipo mubwerere nane pamodzi, kuti ndikampembedze Chauta.” Koma Samuele adayankha kuti, “Sindibwerera nanu, popeza kuti mwakana mau a Chauta, Iyenso wakukanani kuti musakhalenso mfumu yolamulira Aisraele.” Pamene Samuele ankatembenuka kuti azipita, Saulo adagwira mpendero wa mkanjo wake, ndipo mkanjowo udang'ambika. Apo Samuele adamuuza kuti, “Chauta wachita ngati kung'amba ufumu wa Israele kuchoka kwa inu lero, ndipo waupereka kwa mnzanu wabwino koposa inuyo. Mulungu Waulemerero wa Aisraele sanama kapena kusintha maganizo. Pakuti Iye si munthu, kuti athe kusintha maganizo.” Tsono Saulo adati, “Inde ndachimwa, komabe chonde mundilemekeze pakati pa atsogoleri a anthu anga ndi pamaso pa Aisraele onse, ndipo mubwerere nane pamodzi, kuti ndikapembedze Chauta, Mulungu wanu.” Choncho Samuele adabwereradi, natsagana ndi Saulo. Ndipo Sauloyo adapembedza Chauta. Pambuyo pake Samuele adauza Saulo kuti, “Bwera nayeni kuno Agagi uja, mfumu ya Aamaleke.” Ndipo Agagiyo adafika kwa Samuele mokondwa, chifukwa adati, “Ndithudi, zoŵaŵa za imfa zapita!” Koma Samuele adati, “Monga momwe lupanga lako lasandutsira akazi kuti akhale opanda ana, momwemonso mai wako adzakhala wopanda mwana pakati pa akazi ena.” Ndipo Samuele adapha Agagiyo namduladula patsogolo pa guwa la Chauta ku Giligala. Tsono Samuele adapita ku Rama, koma Saulo adapita ku nyumba yake ku Gibea wa Saulo. Samuele sadamuwonenso Saulo moyo wake wonse, koma ankamulira ndithu, popeza kuti Chauta adaamuchotsa Sauloyo kukhala mfumu yolamulira Aisraele. Chauta adauza Samuele kuti, “Kodi udzakhala ukumlirabe Saulo mpaka liti, poti ndamkana kuti asakhalenso mfumu yolamulira Aisraele? Dzaza mafuta m'nsupa yakoyi. Upite kwa Yese wa ku Betelehemu, poti ndadzipezera mfumu pakati pa ana ake aamuna.” Samuele adafunsa Chauta kuti, “Kodi ndingathe bwanji kupitako? Saulo akamva zimenezi, adzandipha.” Chauta adati, “Utenge ng'ombe yaikazi popita, ndipo ukanene kuti, ‘Ndadzapereka nsembe kwa Chauta.’ Uitane Yese kunsembeko, tsono Ine ndikakulangiza zoti ukachite. Ukandidzozere amene ndikakutchulire.” Samuele adachitadi zimene Chauta adalamula, nakafika ku Betelehemu. Atsogoleri amumzindamo adadzamchingamira ali njenjenje, ndipo adamufunsa kuti, “Kodi nkwabwino?” Samuele adayankha kuti, “Inde, nkwabwino. Ndadzapereka nsembe kwa Chauta. Mudzipatule, ndipo mupite nane kukapereka nsembe.” Pamenepo Samuele adapatula Yese ndi ana ake aamuna, ndipo adaŵaitana kuti akapereke nao nsembe. Onsewo atafika, Samuele adayang'ana Eliyabu namaganiza kuti, “Ndithudi amene Chauta adamsankha ndi uyu ali pamaso pakeyu.” Koma Chauta adauza Samuele kuti, “Usayang'ane maonekedwe ake, ngakhale kutalika kwa msinkhu wake, poti ndamkana ameneyo. Chauta sapenya monga m'mene apenyera anthu. Anthu amapenya zakunja, koma Chauta amapenya zamumtima.” Tsono Yese adaitana Abinadabu namtumiza kwa Samuele. Ndipo Samuele adati, “Ameneyunso Chauta sadamsankhe.” Pamenepo Yese adaitana Sama kuti apite kwa Samuele. Koma Samuele adati, “Ameneyunso Chauta sadamsankhe.” Choncho Yese adatumiza ana ake aamuna asanu ndi aŵiri kuti apite kwa Samuele. Koma Samueleyo adati, “Chauta sadaŵasankhe ameneŵa.” Tsono adafunsa Yese kuti, “Kodi ana ako aamuna ndi okhaŵa?” Yeseyo adati, “Alipo wina wamng'ono, mzime, amene watsala, koma iyeyo akuŵeta nkhosa.” Apo Samuele adauza Yese kuti, “Mtumireni munthu, akamtenge, pakuti sitipereka nsembe mpaka iyeyo atabwera pano” Choncho adatuma munthu kukamtenga, ndipo adabwera naye. Anali wofiirira ndi wa maonekedwe okongola ochititsa kaso. Pamenepo Chauta adati, “Ndi ameneyu, mdzoze.” Samuele adatenga nsupa ya mafuta, namdzoza pamaso pa abale ake. Ndipo mzimu wa Chauta udamloŵa Davide mwamphamvu kuyambira tsiku limenelo mpaka m'tsogolo mwake. Pambuyo pake Samuele adanyamuka napita ku Rama. Nthaŵi imeneyo mzimu wa Chauta udaamchokera Saulo ndipo mzimu wina woipa, wotumidwa ndi Chauta, udayamba kumzunza. Atumiki ake adamuuza kuti, “Onani, tsopano mzimu woipa, wotumidwa ndi Mulungu, ukukuzunzani. Ndiye inu mbuyathu, tilamuleni antchito anufe pano kuti tifunefune munthu waluso poimba zeze. Mzimu woipawu ukakufikirani, munthuyo azidzaimba zeze, ndipo mudzapeza bwino.” Pamenepo Saulo adaŵauza kuti, “Chabwino mundifunire munthu wodziŵa bwino kuimba kwake, ndipo mubwere naye kuno.” Mmodzi mwa antchitowo adati, “Ndaona mwana wamwamuna wa Yese wa ku Betelehemu amene ali wokhoza zeze, munthu wolimba mtima, ngwazi pankhondo, wochenjera polankhula, munthu wokongola. Ndipo Chauta ali naye.” Choncho Saulo adatuma amithenga kwa Yese kukanena kuti, “Tumizire Davide mwana wako, uja amaŵeta nkhosayu.” Yese adatenga bulu namsenzetsa buledi, thumba lachikopa la vinyo ndi mwanawambuzi. Zonsezo adapatsa Davide mwana wake, kuti akazipereke kwa Saulo. Motero Davide adafika kwa Saulo, nayamba ntchito yake yomtumikira. Saulo adamkonda kwambiri, namsandutsa wonyamula zida zake zankhondo. Kenaka Saulo adatumiza mau kwa Yese kuti, “Davide akhale womanditumikira, pakuti ndamkonda kwambiri.” Tsono nthaŵi zonse mzimu woipa uja ukamfikira Saulo, Davide ankatenga zeze namamuimba. Motero Saulo ankapeza bwino, ndipo mzimu woipawo unkamsiya. Afilisti adasonkhanitsa magulu ao ankhondo ku Soko, m'dziko la Yuda. Adamanga zithando zao pakati pa Soko ndi Azeka ku Efesi-Damimu. Saulo adasonkhanitsa Aisraele, namanga zithando zao zankhondo m'chigwa cha Ela, nandanditsa gulu lankhondo kuti amenyane ndi Afilistiwo. Afilisti ndi Aisraele adaika ankhondo ao moyang'anana, ena mbali ina paphiri, ena mbali ina paphirinso, pakatipa chigwa. Tsono ku zithando za Afilisti kudatuluka munthu wina wamphamvu wa ku Gati, dzina lake Goliyati. Msinkhu wake unali pafupi mamita atatu. Ankavala chisoti chamkuŵa ndi malaya achitsulo, amene kulemera kwake kunali ngati makilogramu 57. Ankavalanso zokuta miyendo yake zamkuŵa, ndipo ankanyamula nthungo yamkuŵa pa phewa. Thunthu la mkondo wake linali ngati mtanda wa choombera nsalu. Mutu wa nkhondowo unkalemera ngati makilogramu asanu ndi aŵiri. Patsogolo pake pankapita munthu womunyamulira chishango. Goliyatiyo adaimirira ndi kufuula kwa ankhondo a Aisraele kuti, “Chifukwa chiyani mukuchita kukonzekera nkhondo chotere? Ineyo ndine Mfilisti, inuyo ndinu akapolo a Saulo. Bwanji osati mungosankhula munthu pakati panupo, adze kwa ine. Ngati angathe kulimbana nane ndi kundipha, ndiye kuti Afilisti tonse tidzakhala akapolo anu. Koma ndikampambana ndi kumupha, inuyo mudzakhala akapolo athu ndi kumatigwirira ntchito. Tiwonane lero lino basi! Patseni munthu kuti ndimenyane naye.” Atamva mau a Mfilistiyo, Saulo ndi Aisraele onse adachita mantha nathyoka m'nkhongono. Davide anali mwana wa Mwefurati wa ku Betelehemu dzina lake Yese, amene anali ndi ana aamuna asanu ndi atatu. Pa nthaŵi ya ufumu wa Saulo, Yese anali atakalamba kale kwambiri. Ana ake aamuna anali aŵa: Eliyabu mwana wake wachisamba, wachiŵiri Abinadabu, ndipo wachitatu anali Sama. Davide anali mzime. Ana akuluakulu atatuwo ndiwo anali ku nkhondo ndi Saulo. Koma Davide ankapita ku zithando za Saulo, namabwerako nthaŵi zina kukaŵeta nkhosa za bambo wake ku Betelehemu. Pa masiku makumi anai Goliyati uja adakhala akutuluka, namadziwonetsa m'maŵa ndi madzulo. Tsiku lina Yese adauza mwana wake Davide kuti, “Abale ako uŵatengere makilogramu khumi a tirigu wokazinga, ndi mitanda khumi yabulediyi, ndipo upite nazo mofulumira ku zithando zao. Utengenso mphumphu khumizi za tchizi, upite nazo kwa mkulu wolamulira ankhondo. Ukaone m'mene abale ako akukhalira, ndipo ubwereko ndi chizindikiro china chosonyeza kuti ali bwino. Saulo, abale akowo ndi Aisraele ena, akumenyana nkhondo ndi Afilisti ku chigwa cha Ela.” Tsono Davide adanyamuka m'mamaŵa, nasiyira nkhosa munthu wina wozisunga. Adatenga zakudyazo napita, monga momwe bambo wake adaamlamulira. Adafika ku zithando pamene ankhondo ankandanda pa mzere wankhondo, nkufuula mfuu wankhondo. Aisraele ndi Afilisti adaandanda pa mzere wankhondo moyang'anana. Tsono zakudya zija Davide atasiyira munthu wosunga katundu, adathamangira kumene kunali ankhondo, nakalonjera abale ake. Pamene ankalankhula ndi abale akewo, adangoona Goliyati uja akutuluka ku magulu ankhondo a Afilisti, akulankhula zonyoza zomwe zija. Davide nkumva zimenezo. Aisraele onse atamuwona munthuyo, adathaŵa chifukwa ankamuwopa kwambiri. Ankati, “Muwonenitu munthu uja! Amangobwera, amangodzatinyoza Aisraelefe. Tsono amene amuphe, mfumu idati idzampatsa chuma chambiri, adzampatsanso mwana wake wamkazi kuti amkwatire. Banja la bambo wake silidzalipiranso msonkho.” Tsono Davide adafunsa anthu amene anali pafupi naye kuti, “Adzamtani munthu amene adzaphe Mfilistiyu ndi kuŵachotsa manyazi Aisraele? Mfilisti wosaumbalidwayu ndaninso kuti angamanyoze ankhondo a Mulungu wamoyo?” Anthu adamuuzanso zomwe zija zimene mfumu idaati idzachitire munthu wodzapha Goliyatiyo. Eliyabu, mkulu wake, atamva Davideyo akulankhula ndi anthu, adamupsera mtima, namufunsa kuti, “Wadzachita chiyani kuno? Nanga nkhosa zija wasiyira yani ku chipululu? Ndikudziŵa kuti ndiwe wodzikuza ndi woipa mtima. Wadza kuno kudzangoona nkhondo chabe!” Davide adati, “Kodi ndachimwa chiyani? Ndiye kuti ndileke nkulankhula komwe?” Tsono adachoka apo napita kwa wina namufunsa zokhazokhazo. Aliyense adamuyankhanso monga poyamba paja. Mau amene ankalankhula Davide aja atamveka, anthu adakafotokozera Saulo, ndipo Sauloyo adamuitanitsa. Tsono Davide adauza Saulo kuti, “Munthu aliyense asataye mtima chifukwa cha Mfilistiyu. Ineyo mnyamata wanune ndipita kukamenyana naye.” Saulo adamuuza kuti, “Sungathe kukamenyana naye Mfilistiyu, pakuti iwe ndiwe mnyamata, koma iyeyu ndi munthu wozoloŵera kumenya nkhondo kuyambira ubwana wake.” Apo Davide adauza Saulo kuti, “Mnyamata wanune ndinkaŵeta nkhosa za bambo wanga. Ndipo mkango ukafika, kapena chimbalangondo, ndi kugwira mwanawankhosa pakati pa nkhosazo, ndinkalondola mpaka kuchipha chilombocho ndi kupulumutsa mwanawankhosayo kukamwa kwake. Ndipo chikati chindiwukire, ndinkachigwira tchoŵa lake ndi kuchikantha mpaka kuchipha. Ineineyo ndidaphapo mikango ndi zimbalangondo zomwe. Tsono Mfilisti wosaumbalidwayu, ndidzamupha monga momwe ndidaphera zilombo zija, popeza kuti akunyoza magulu ankhondo a Mulungu wamoyo. Chauta amene adandipulumutsa ku mkango ndi ku chimbalangondo, adzandipulumutsa kwa Mfilistiyu.” Apo Saulo adauza Davide kuti, “Pita, Chauta akhale nawe.” Tsono Saulo adaveka Davide zovala zake zankhondo. Adamveka chisoti chamkuŵa ndi malaya achitsulo. Kenaka Davide adamanga lupanga m'chiwuno mwake. Atayesera kuyenda, adaona kuti akulephera poti sadazoloŵere. Ndiye adauza Saulo kuti, “Sindingathe kuyenda nazo, poti sindidazoloŵere.” Choncho adavula zovalazo. Tsono adatenga ndodo yake m'manja. Adatola miyala isanu yosalala yakumtsinje, naiika m'thumba lake lakubusa. Ali ndi khwenengwe m'manja, adapita kukakumana ndi Mfilisti uja. Tsono Mfilistiyo adayambapo kupita kumene kunali Davide, munthu wonyamula chishango ali patsogolo pake. Ndipo atayang'ana Davideyo, adayamba kumnyoza, poona kuti anali mnyamata chabe, wofiirira ndiponso wa maonekedwe okongola. Tsono adafunsa Davide kuti, “Kodi ndine galu, kuti uzibwera kwa ine ndi ndodo?” Pompo adayamba kutemberera Davide potchula milungu yake. Kenaka adauza Davide kuti, “Idza kuno, mnofu wako ndidyetsera mbalame zamumlengalenga ndi zilombo zakuthengo.” Koma Davide adauza Mfilistiyo kuti, “Wadza kwa ine ndi lupanga, mkondo ndi nthungo. Koma ine ndikudza kwa iwe m'dzina la Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa magulu ankhondo a Aisraele, amene iwe wamunyoza. Lero lomwe lino Chauta akupereka m'manja mwanga. Ndikulasa ndi kukugwetsa pansi, ndipo ndikudula mutu. Mitembo ya magulu ankhondo a Afilisti ndiipereka lero lino kwa mbalame zamumlengalenga, ndi kwa zilombo zakuthengo, kuti dziko lonse lapansi lidziŵe kuti kuli Mulungu ku dziko la Israele. Anthu onse amene asonkhanaŵa adzadziŵa kuti Chauta sapulumutsa anthu ndi lupanga kapena mkondo wokha. Wopambanitsa pa nkhondo ndi Chauta, ndipo akuperekani m'manja mwathu.” Tsono Mfilistiyo adasendera pafupi kuti akumane ndi Davide. Pomwepo Davideyo adathamanga mofulumira ku mzere wankhondo uja, kuti nayenso akakumane naye. Adapisa dzanja m'thumba natulutsamo mwala, ndipo adauponya namlasa pa mphumi Mfilistiyo. Mwalawo udamuloŵa m'mutu, ndipo Mfilistiyo adagwa pansi chafufumimba. Choncho Davide adampambana Goliyati uja pomlasa ndi mwala wam'khwenengwe, namupha Mfilistiyo. M'manja mwa Davide munalibe konse lupanga. Pompo adathamanga, nakaimirira pamwamba pa Mfilisti uja. Adasolola lupanga lake lomwe m'chimake, namtsiriza pomdula mutu. Tsono Afilisti ataona kuti ngwazi yao yamphamvu pa nkhondo yafa, adathaŵa. Aisraele ndi anthu a ku dziko la Yuda adanyamuka akufuula, napirikitsa Afilisti aja mpaka ku Gati ndi ku zipata za Ekeroni. Tsono Afilisti ovulala ankagwa pa njira yonse kuyambira ku Saraimu mpaka ku Gati ndi Ekeroni. Ndipo Aisraele adabwererako kumene ankapirikitsa Afilisti kuja, nadzafunkha m'zithando zankhondo za Afilistiwo. Kenaka Davide adatenga mutu wa Mfilisti uja napita nawo ku Yerusalemu. Koma zida zokha za Mfilistiyo adaziika m'hema mwake. Pamene Saulo adaaona Davide akupita kukamenyana ndi Mfilisti uja, adafunsa Abinere mkulu wa ankhondo kuti, “Kodi iwe Abinere, mnyamatayu ndi mwana wa yani?” Abinere adayankha kuti, “Pepani inu amfumu muli apa, ine sindingadziŵe.” Apo mfumu idati, “Kafunse kuti kodi mnyamata ameneyu ndi mwana wa yani?” Tsono pamene Davide ankabwererako kumene adaakapha Mfilisti kuja, Abinere adamtenga napita naye kwa Saulo, mutu wa Mfilisti uja uli m'manja mwake. Saulo adafunsa Davide kuti, “Kodi mnyamata iwe, paja ndiwe mwana wa yani?” Davide adayankha kuti, “Ndine mwana wa mtumiki wanu Yese, wa ku Betelehemu.” Davide atatha kulankhula ndi Saulo, mtima wa Yonatani udagwirizana ndi mtima wa Davide, ndipo Yonatani adakonda Davideyo monga momwe ankadzikondera iye mwini. Mwakuti adamtenga Davideyo tsiku lomwelo, osamlola kuti abwerere ku banja kwa bambo wake. Adachita naye chipangano chifukwa ankamkonda monga momwe ankadzikondera iye mwini. Tsono adavula mwinjiro umene anali nawo napatsa Davide pamodzi ndi zovala zankhondo, lupanga lake, uta wake ndi lamba wake. Tsono kulikonse kumene Davide ankatumidwa ndi Saulo kuti akamenye nkhondo, ankapambana adani. Motero Saulo adamuika Davide kuti akhale mtsogoleri wa ankhondo. Chimenechi chidakondwetsa anthu onse, ngakhalenso atsogoleri a ankhondo a Saulo. Pamene anthu ankabwerera kwao, Davide atapha Mfilisti uja, akazi adatuluka m'mizinda yonse ya Aisraele akuimba ndi kuvina, kuti achingamire mfumu Saulo. Ankaimba ndi kumavina mokondwa, kwinaku ng'oma ndi zitoliro zikugundika. Akaziwo ankapolokezana akukondwerera namati, “Saulo wapha zikwi inde, koma Davide wapha zikwi khumikhumi!” Apo Saulo adapsa mtima kwambiri, mau ameneŵa adaipidwa nawo. Adati, “Davide amuŵerengera zikwi zochuluka, koma ine andiŵerengera zikwi zochepa. Nanga chamkhaliranso nchiyani? Si ufumu basi?” Motero Saulo ankamuwona ndi diso loipa Davide kuyambira tsiku limenelo. M'maŵa mwake mzimu woipa uja udamtsikira Saulo, ndipo adayamba kubwebweta moyaluka m'nyumba mwake. Davide ankamuimbira zeze, monga momwe ankachitira tsiku ndi tsiku. Saulo anali ndi mkondo m'manja mwake. Tsono adaponya mkondowo ndipo mumtima mwake adati, “Ndimubaya ndi kumkhomera ku chipupa.” Koma Davide adauleŵa. Zidachitika kaŵiri konse. Pambuyo pake Saulo adayamba kuwopa Davide, chifukwa choti tsopano Chauta anali ndi Davide, kumsiya iyeyo. Motero Saulo adamtuma Davide kwina kwake, ndipo adamuika kuti akhale mtsogoleri wa ankhondo 1,000. Davide ankapita namabwera akuŵatsogolera. Ndipo ankapambana pa zonse zimene ankachita, chifukwa Chauta anali naye. Tsono pamene Saulo adaona kuti Davide akupambana kwambiri, adayamba kuchita naye mantha. Koma anthu onse a ku Israele ndi a ku Yuda ankamkonda Davide, chifukwa iyeyu ankaŵatsogolera namapambana pa zonse. Tsiku lina Saulo adauza Davide kuti, “Nayu Merabi mwana wanga wamkulu. Ndidzakupatsa kuti akhale mkazi wako. Koma unditumikire molimba mtima pomenya nkhondo za Chauta.” Potero Saulo ankaganiza kuti, “Ndisamuphe ndine ndi dzanja langa, koma amuphe ndi Afilisti.” Tsono Davide adafunsa Saulo kuti, “Kodi ine ndine yani, ndipo abale anga ndi banja la bambo wanga ndife yani m'dziko la Israele, kuti ine nkukhala mkamwini wa mfumu?” Koma pa nthaŵi yoti Merabi, mwana wa Saulo, akwatiwe ndi Davide, bambo wake adampereka kwa Adriyele Mmehola, kuti akhale mkazi wake. Komabe Mikala, mwana wina wamkazi wa Saulo, ankakonda Davide. Saulo atamva, adakondwa kwambiri. Adaganiza kuti, “Ndimpatse amkwatire, kuti adzakhale ngati msampha kwa Davideyo, ndipo Afilisti adzamupha.” Nchifukwa chake Saulo adauza Davide kachiŵiri kuti, “Tsopano udzakhala mkamwini wanga.” Motero adalamula nduna zake kuti, “Mulankhule naye Davide pambali nkumuuza kuti, ‘Mfumu imakukonda, ndipo ngakhale nduna zake zimakukonda. Tsono ukhale mkamwini wa mfumu.’ ” Nduna za Saulo zidamuuza Davide mau amenewo. Koma iye adati, “Kani mukuchiyesa chinthu chapafupi kukhala mkamwini wa mfumu? Kodi simukuwona kuti ndine wosauka ndi wosatchuka?” Nduna za Saulo zidamuuza zonse zimene Davide adaanena. Tsono Saulo adati, “Kamuuzeni kuti, sindikufuna chiwongo cha mtundu uliwonse ai, ndingofuna timakungu ta nsonga za mavalo a Afilisti 100, kuti ndilipsire adani anga.” Potero Saulo ankaganiza zoti Davide aphedwe ndi Afilisti. Ndiye nduna za Saulozo zitamuuza Davide mau ameneŵa, zidamkondweretsa kuti akhale mkamwini wa mfumu. Nthaŵi yoti atenge mkazi wake isanakwane, Davide adanyamuka napita pamodzi ndi ankhondo ake, ndipo adakapha Afilisti 200. Adabwera nato timakungu tija natipereka kwa mfumu, kuti choncho akhale mkamwini wake. Apo Saulo adapatsa Davideyo mwana wake Mikala, kuti akhale mkazi wake. Koma Saulo atazindikira kuti Chauta ali naye Davide, ndiponso kuti mwana wake Mikala ankamkonda Davideyo, adamuwopabe kwambiri ndi kudana naye moyo wake wonse. Tsono pamene Afilisti ankatuluka kukamenya nkhondo, nthaŵi zonse Davide ankapambana kwambiri kuposa atsogoleri ena onse a ankhondo a Saulo. Choncho dzina lake la Davide lidatchuka kwambiri. Saulo adalamula mwana wake Yonatani ndi akuluakulu onse kuti aphe Davide. Koma Yonatani ankakonda Davide kwambiri. Choncho adakauza Davide kuti, “Iwe, abambo anga akufuna kukupha. Ndiye uchenjere, m'maŵa ukakhale kwina kobisalika. Ine ndidzapita ndi kukaima pakhundu pa bambo wanga kuminda kumene iwe ukabisaleko, tsono ndidzalankhula ndi bambo wanga za iwe. Chilichonse chimene ndidzamve, ndidzakuuza.” Tsono Yonatani adaterodi ndipo adakanena zabwino za Davide kwa bambo wake, namuuza kuti, “Atate, musachimwire mtumiki wanu Davide, poti sadakuchimwireni, koma amakuchitirani zabwino. Paja adaaika moyo wake pa minga pakupha Goliyati Mfilisti uja. Pambuyo pake Chauta adachita zazikulu pakupambanitsa Aisraele pa nkhondo. Inu mudaona zimenezo ndi kukondwera nazo. Chifukwa chiyani tsono mukufuna kuchimwira munthu wosalakwa, pofuna kumupha Davideyu?” Saulo adamvera mau a Yonatani, ndipo adalumbira kuti, “Mulungudi! Davideyo sadzaphedwa!” Tsono Yonatani adaitana Davide namuuza zonsezo. Choncho Yonatani adabwera naye kwa Saulo, ndipo Davideyo ankatumikira Saulo monga kale. Nkhondo ina idabukanso. Davide adapita kukamenyana ndi Afilisti. Adapha Afilisti ambiri, kotero kuti iwowo adathaŵa. Tsiku lina mzimu woipa uja udatsikira Saulo pa nthaŵi yomwe anali m'nyumba mwake, mkondo uli m'manja, Davide akuimba zeze. Pomwepo Saulo adayesa kubaya Davide ndi kumkhomera ku chipupa. Koma Davide adauleŵa mkondowo, kotero kuti udangolasa chipupa. Ndipo adathaŵa napulumuka. Usiku womwewo Saulo adatuma anthu kunyumba kwa Davide kuti akambisalire, kuti choncho akamuphe Davide m'maŵa. Koma Mikala, adauza mwamuna wake Davide kuti, “Mukapanda kupulumutsa moyo wanu usiku uno, maŵa muphedwa.” Choncho Mikala adamtulutsira Davideyo pa windo, ndipo adathaŵa. Mikalayo adatenga fano lam'nyumba naligoneka pa bedi, naika mtsamiro wa ubweya wambuzi kumutu kwake kwa fanolo, nalifunditsa nsalu. Pamene anthu a Saulo aja adafika kuti adzamgwire Davide, Mikala adati, “Davide akudwala.” Koma Saulo adaŵatumanso anthuwo kuti akamgwire ndithu Davideyo. Adaŵauza kuti, “Mubwere naye kuno, mumnyamulire pabedi pomwepo kuti ndidzamuphe.” Anthuwo atakaloŵa, adangoona fano pabedipo ndi mtsamiro wa ubweya wambuzi kumutu kwake kwa fanolo. Atamva zimenezi Saulo adafunsa Mikala kuti, “Chifukwa chiyani wandinyenga chotere pa kulola kuti mdani wanga athaŵe?” Mikala adayankha kuti, “Davide adaandiwuza kuti, ‘Undilole ndipite. Ngati sutero, ndikupha.’ ” Choncho Davide adathaŵa napulumuka, nakafika kwa Samuele ku Rama. Adafotokozera Samuele zonse zimene Saulo adamuchita. Tsono Davideyo pamodzi ndi Samuele adakakhala ku Nayoti. Saulo atamva kuti Davide ali ku Nayoti ku Rama, pompo adatumanso anthu kuti akamgwire. Anthuwo adaona gulu la aneneri akuvina namalosa, Samuele akuŵatsogolera. Pamenepo mzimu wa Mulungu udaŵaloŵa anthuwo ndipo nawonso adayamba kulosa. Saulo atazimva zimenezo, adatuma anthu ena, ndipo nawonso adayamba kulosa. Adatumanso anthu ena kachitatu, nawonso adayamba kulosa. Choncho Saulo mwini wake adanyamuka napita ku Rama, nakafika pa chitsime chachikulu chimene chili ku Seku. Ndipo adafunsa kuti, “Kodi Samuele ndi Davide ali kuti?” Munthu wina adati, “Ali ku Nayoti ku Rama.” Saulo adachoka napita ku Nayoti ku Rama. Nayenso mzimu wa Mulungu udamloŵa ndipo ankayenda akuvina namalosa mpaka kukafika ku Nayoti ku Rama. Nayenso adavula zovala zake namalosa pamaso pa Samuele, kenaka nkugona chamaliseche tsiku lonse, usana ndi usiku. Choncho padayambika chisudzo chakuti, “Kani Saulonso ali m'gulu la aneneri?” Tsono Davide adathaŵa ku Nayoti ku Rama, nabwera kwa Yonatani. Ndipo adafunsa Yonatani kuti, “Kodi ndidachita chiyani? Ndidalakwa chiyani? Kodi abambo ako ndidaŵachimwira chiyani, kuti azifuna kundipha?” Yonatani adamuuza kuti, “Sizingatero, suufa ai. Abambo anga sachita chilichonse, chachikulu kapena chaching'ono, osandiwuza. Tsono abambo anga angandibisire bwanji zimenezi? Si choncho ai.” Koma Davide adalumbira kuti, “Abambo ako akudziŵa bwino lomwe kuti umandikonda, ndipo adati, ‘Yonatani asadziŵe zimenezi kuwopa kuti angamve chisoni.’ Koma ndithu, Mulungudi, iwe Yonatani uli apa, imfa sili nane kutali.” Apo Yonatani adauza Davide kuti, “Chilichonse chimene unene, ndidzakuchitira.” Davide adati, “Paja maŵa kuli phwando la mwezi wokhala chatsopano, ndipo sindiyenera kulephera kukadya ndi mfumu. Koma undilole ndipite kuti ndikabisale ku thengo mpaka mkucha madzulo. Abambo ako akandifuna, uŵauze kuti, ‘Davide adandiwumiriza kuti ndimlole kuti athamangire ku mzinda wakwao ku Betelehemu. Akuti kumeneko kuli nsembe yapachaka ya banja lonse.’ Akati, ‘Chabwino’, zinthu zidzandiyendera bwino, ine kapolo wako. Koma akakhala wokwiyabe, udziŵe kuti watsimikiza mtima kuti andichita choipa. Nchifukwa chake undikomere mtima, poti udachita chipangano ndi ine kapolo wako pamaso pa Chauta. Koma ngati ndalakwa, undiphe ndiwe osati ukanditule kwa abambo ako.” Yonatani adati, “Ai, bwanawe, nchosatheka! Ndikadadziŵa kuti abambo anga adatsimikiza zoti akuchite choipa, kodi sindikadakuuza?” Apo Davide adafunsa Yonatani kuti, “Kodi ndani amene adzandiwuze, abambo ako akakuyankha mokalipa?” Yonatani adayankha kuti, “Tiye tikayende chakumindaku.” Choncho onse aŵiriwo adapita kumeneko. Kumindako Yonatani adauza Davide kuti, “Chauta, Mulungu wa Aisraele, akhale mboni. Nditaŵafunsa abambo anga nthaŵi yonga yomwe ino maŵa, ngakhale mkucha, ndipo ndikapeza kuti akufuna kukuchitira chinthu chabwino, ndidzatumiza mau kuti udziŵe. Koma akakafunitsitsa kukuchita choipa, Chauta adzandilange kwambiri ndikapanda kukuululira ndi kukuthandiza kuti upulumuke. Chauta akhale nawe, monga momwe adakhalira ndi abambo anga. Ndikakhala ndili moyobe, udzandiwonetse kukoma mtima konga kwa Chauta. Koma ndikafa, usadzaleke kuchitira chifundo banja langa mpaka muyaya. Pamene Chauta adzaŵatha adani onse a Davide pa dziko lapansi, banja la ine Yonatani lisadzafafanizike nao. Ndithu Chauta alipsire pa adani ake a Davide.” Apo Yonatani adalumbiritsanso Davide kuti asaleke kumkonda, pakuti Yonatani ankakonda Davide monga momwe ankadzikondera iye mwini. Tsono Yonatani adatinso, “Maŵa mwezi ukhala, ndipo pa phwando adzazindikira kuti iwe palibe, popeza kuti pampando pako padzakhala popanda munthu. Mkucha adzakufunanso kwambiri. Tsono udzapite ku malo amene udaabisala tsiku lijali, ndipo ukakhale pa mbali ina ya mulu wa miyala uli apowo. Ine ndidzaponya mivi itatu ku mbali ina ya muluwo, ngati ndikuchita chandamale. Tsono ndidzatuma mnyamata wanga kuti akatole miviyo. Mnyamatayo ndikamuuza kuti, ‘Mivi ili chakuno, kaitole!’ Pomwepo iweyo udzatuluke, chifukwa ndikulumbira, pali Chauta wamoyo, kuti kuli mtendere, iwe sudzakhala pa zoopsa. Koma ndikamuuza mnyamatayo kuti, ‘Mivi ili patsogolo pako,’ pomwepo iweyo uchoke, pakuti Chauta ndiye wati uchokepo. Tsono pa zimene tapanganazi, Chauta ndiye mboni pakati pa ine ndi iwe mpaka muyaya.” Choncho Davide adakabisala ku minda. Ndipo pamene mwezi udaoneka, mfumu Saulo adabwera ku phwando. Adakhala pa mpando wake pafupi ndi khoma, monga m'mene ankachitira nthaŵi zonse. Yonatani adakhala popenyana naye, ndipo Abinere adakhala pambali pa mfumu Saulo, koma pa malo a Davide panalibe munthu. Koma Saulo sadanene kanthu kalikonse tsiku limenelo. Ankaganiza kuti, “Chinthu china chamgwera Davide, mwina mwake ngwosayenera zachipembedzo.” Koma pa tsiku lachiŵiri la phwandolo, pa malo a Davide panalibenso munthu. Ndiye Saulo adafunsa Yonatani kuti, “Chifukwa chiyani Davide mwana wa Yese sadabwere ku phwando dzulo ngakhalenso lero?” Yonatani adayankha kuti, “Davide adandipempha mondiwumiriza kuti ndimlole apite ku Betelehemu. Adati, ‘Undilole ndipite, popeza kuti banja lathu likupereka nsembe mumzindamo, ndipo mbale wanga adandikakamiza kuti ndikakhale nao kumeneko. Tsono ngati wandikomera mtima, undilole ndipite, kuti ndikaone abale anga.’ Nchifukwa chake sadabwere ku chakudya cha mfumu.” Apo Saulo adapsera mtima Yonatani kwambiri, ndipo adamuuza kuti, “Iwe mwana wobadwa kwa chimkazi chapakamwa, kodi ukuyesa kuti sindikudziŵa ine kuti ukugwirizana ndi mwana wa Yese, amene afuna kukuchititsa manyazi iwe ndi mai wakoyo? Kodi sukudziŵa kuti mwana wa Yese akakhalabe ndi moyo pa dziko lapansi, iweyo sudzakhala mfumu? Nchifukwa chake tsono, tuma anthu kuti akamtenge, abwere naye kuno, pakuti ndithudi adzafa.” Yonatani adafunsa bambo wake kuti, “Kodi chifukwa chiyani mufuna kumupha Davide? Kodi walakwa chiyani?” Atamva zimenezi Saulo adamponyera mkondo Yonataniyo kuti amuphe. Pamenepo Yonatani adadziŵa kuti bambo wake watsimikizadi mtima kuti aphe Davide. Tsono Yonatani adanyamuka pa tebulo atakwiya koopsa, ndipo pa tsiku lachiŵiri la phwandolo sadadye. Adaavutika kwambiri mumtima mwake, chifukwa choti bambo wake adaachita Davide chipongwe. M'maŵa mwake Yonatani ndi mnyamata wake adapita kuminda kuja kumene adaapangana ndi Davide. Adauza mnyamata wake kuti, “Thamanga, ukatole mivi imene nditi ndiponye.” Mnyamata uja akuthamanga, Yonatani adaponya muvi patsogolo pa mnyamatayo. Ndipo mnyamatayo atafika pamalo pomwe padaagwa muviwo, Yonatani adanena chokweza kuti, “Muvi uli patsogolo pakopo.” Apo Yonatani adaitananso mnyamatayo nati, “Fulumira, yenda msanga, usachedwe.” Motero mnyamata uja adatola muviwo, nabwera kwa mbuyake. Koma mnyamatayo sadadziŵe kanthu ai, Yonatani yekha ndi Davide ndiwo amene ankadziŵa zimene zinkachitika. Choncho Yonatani adapereka zida zake kwa mnyamata wake uja, namuuza kuti, “Pita, kazitule ku mzinda.” Tsono mnyamatayo atapita, Davide adatulukira ku mbali ina ya mulu wa miyala uja, ndipo adadzigwetsa pansi nagunditsa nkhope yake pansi katatu. Adampsompsonana, nayamba kulira onse aŵiriwo, koma Davide adalira koposa. Pamenepo Yonatani adauza Davide kuti, “Pita ndi mtendere, pakuti aŵirife tidalonjezana molumbira m'dzina la Chauta kuti, ‘Chauta ndiye adzakhale mboni pakati pa ine ndi iwe, ndi pakati pa zidzukulu zanga ndi zidzukulu zako mpaka muyaya.’ ” Pompo Davide adanyamuka nachokapo, ndipo Yonatani adabwerera kumzinda kuja. Davide adakafika ku Nobu kwa wansembe Ahimeleki. Ahimelekiyo adadzamchingamira akunjenjemera, namufunsa kuti, “Zatani kuti muli nokha popanda ndi mmodzi yemwe wokuperekezani?” Davide adayankha kuti, “Mfumu yandituma ndipo yandilamula kuti ndisauze munthu wina aliyense zimene yanditumazo. Kunena za anthu anga, ndapangana nawo kuti tikakumane pa malo ena ake. Kodi muli ndi chakudya? Mundipatseko mitanda isanu yabuledi kapena chakudya chilichonse chimene muli nacho pano.” Wansembeyo adayankha kuti, “Pano ndilibe buledi wamba, koma alipo ndi buledi wachipembedzo. Ngati anthu anu sadakhale ndi akazi ao, angathe kudya.” Davide adayankha kuti, “Kunena zoona, nthaŵi zonse tikakhala pa ulendo, timakhala odzimanga. Anthu anga amakhala odzimanga ngakhale pa ulendo wamba, nanji lero pamene tili pa ulendo woterewu!” Apo wansembeyo adapereka buledi wachipembedzo kwa Davide, pakuti kunalibe buledi wina, koma buledi yekha woperekedwa kwa Chauta. Buledi wake ndi amene anali atamchotsa pamaso pa Chauta kuti akaikepo wina wamoto. Tsiku limenelo munthu wina mwa antchito a Saulo anali pomwepo, pakuti adaayenera kuchita mwambo wachipembedzo ku nyumba ya Chauta. Munthuyo dzina lake anali Doegi Mwedomu, kapitao wa abusa a Saulo. Davide adafunsa Ahimeleki kuti, “Kodi kulibe mkondo kuno kapena lupanga? Paja ine sindidabwere ndi lupanga langa kapena zida zanga chifukwa ntchito ya mfumuyo inali yofulumira.” Wansembeyo adayankha kuti, “Lupanga la Goliyati Mfilisti uja amene mudamupha ku chigwa cha Ela, nlokulunga m'nsalu paseli pa chovala cha efodi. Ngati mufuna, mungathe kutenga limenelo, chifukwa kulibenso lina kuno, koma lokhalo.” Davide adati, “Palibe lina lofanafana ndi limenelo. Patseni lomwelo.” Tsiku lomwelo Davide adanyamuka kuthaŵa Saulo, ndipo adapita kwa Akisi mfumu ya ku Gati. Tsono nduna za Akisi zidamufunsa Akisiyo kuti, “Kodi ameneyu si Davide, mfumu ya dziko? Kodi iyeyu si uja pomuvinira ankamuimbira kuti, “ ‘Saulo wapha zikwi, inde, koma Davide wapha zikwi khumikhumi!’ ” Mau ameneŵa Davide adamloŵa mu mtima kwambiri, ndipo adayamba kuwopa Akisi mfumu ya ku Gati. Choncho adasintha khalidwe lake pamaso pao, nadzisandutsa ngati wamisala, namangolembalemba pa zitseko za chipata, malovu ali chuchuchu kutsikira ku ndevu. Tsono Akisi adauza nduna zake kuti, “Mukuwona kuti munthuyu ngwamisala. Chifukwa chiyani tsono mwabwera naye kwa ine? Kodi ndikusoŵa anthu amisala kuti muzibwera naye kuno munthu ameneyu, namachita zamisala zake pamaso panga? Ha! Munthu wotereyu angaloŵe bwanji m'nyumba mwanga muno?” Pamenepo Davide adathaŵa ku Gati, nakabisala ku phanga la Adulamu. Abale ake ndi onse a m'banja la bambo wake atamva, adapita kumene kunali Davide. Tsono aliyense amene anali pa mavuto, kapena anali ndi ngongole, kapena anali wosakondwa, onsewo adasonkhana kwa Davide. Iyeyo ankaŵatsogolera. Onse anali ngati anthu 400 pamodzi. Pambuyo pake Davide adachoka kumeneko, napita ku Mizipa ku Mowabu. Adapempha mfumu ya ku Mowabu kuti, “Chonde, bwanji bambo wanga ndi mai wanga akhale nao kuno, mpaka nditadziŵa zimene Mulungu adzandichitire.” Choncho adaŵasiya kumeneko makolo akewo kwa mfumu ya ku Mowabuko, ndipo iwo adakhala komweko nthaŵi yonse imene Davide ankabisala kuphanga kuja. Tsono mneneri Gadi adauza Davide kuti, “Musakhale pano. Muchoke, mupite ku dziko la Yuda.” Pomwepo Davide adachoka, nakaloŵa m'nkhalango ya Hereti. Tsono Saulo adamva kuti Davide ndi anthu ake adapezeka. Tsiku limenelo Sauloyo adaakhala pansi patsinde pa mtengo wa mbwemba womera pa chitunda china ku Gibea, mkondo uli m'manja, ankhondo ake atamzungulira. Ndiye Sauloyo adafunsa ankhondo ake aja kuti, “Imvani tsono inu Abenjamini. Kodi mwana wa Yese adzakupatsani minda aliyense mwa inu? Kodi adzakusandutsani atsogoleri a magulu ankhondo nonsenu? Mwina nchifukwa chaketu mukundichita chiwembu chotere. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adandiwululira pamene mwana wanga ankagwirizana ndi mwana wa Yese. Palibe ndi mmodzi yemwe amene akulabadako za ine kapena kundinong'onezako kuti mwana wanga wautsa mtima wa munthu wanga Davide kuti andiwukire, monga akuchitira leromu.” Apo Doegi Mwedomu, amene adaaimirira pafupi ndi nduna za Saulo, adanena kuti, “Ine ndidamuwona mwana wa Yese akupita ku Nobu kwa Ahimeleki, mwana wa Ahitubi. Ndipo Ahimelekiyo adafunsa Chauta zimene Davide ankayenera kuchita. Kenaka adampatsa chakudya, nampatsanso lupanga la Goliyati, Mfilisti uja.” Tsono mfumu Saulo adaitanitsa wansembe Ahimeleki, mwana wa Ahitubi, pamodzi ndi onse a m'banja la bambo wake, amene anali ansembe ku Nobu. Onsewo adabwera kwa mfumu. Ndipo Saulo adati, “Imva tsono, iwe mwana wa Ahitubi.” Iye adayankha kuti, “Inde, mbuyanga.” Saulo adamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani wandichita chiwembu iwe ndi mwana wa Yese? Wampatsa buledi ndi lupanga, ndipo wamfunsira kwa Mulungu zoti achite. Taonani, tsopano wandiwukira, ndipo akundilalira lero lino!” Koma Ahimeleki adayankha mofunsa kuti, “Amfumu, kodi ndani pakati pa ankhondo anu amene ali wokhulupirika ngati Davide? Iye uja ndi mkamwini wanu, mtsogoleri wa gulu lanu lokutchinjirizani, ndiponso munthu wolemekezeka m'banja mwanu? Kodi ndayamba lero kumfunsira kwa Mulungu zoti achite? Iyai, amfumu! Musandinenere kanthu kena kalikonse koipa, ine mtumiki wanu, kapenanso wina aliyense wa m'banja la bambo wanga, pakuti sindikudziŵa kanthu pa nkhaniyi mpang'ono pomwe.” Komabe mfumu idati, “Iwe Ahimeleki, ndi onse a m'banja la bambo wako, mufa ndithu nonse!” Tsono idauza alonda omwe anali naye kuti, “Apheni ansembe a Chautaŵa, chifukwa akugwirizana ndi Davide. Adaadziŵa kuti Davideyo adathaŵa, koma sadandiwululire zimenezo.” Koma anyamata a mfumuwo sadasamule manja kuti aphe ansembe a Chauta. Pomwepo mfumu idauza Doegi kuti, “Kaŵaphe ndiwe.” Doegi, Mwedomu uja, adapitadi kukapha ansembewo. Adapha anthu 85 ololedwa kuvala efodi ya thonje lokoma. Kunena za Nobu, mzinda wa ansembe uja, Saulo adalamula kuti anthu onse okhalamo aphedwe. Choncho amuna ndi akazi, ana ndi makanda, kudzanso ng'ombe, abulu ndi nkhosa, zonsezo adazipha ankhondo ake. Koma mmodzi mwa ana aamuna a Ahimeleki, mwana wa Ahitubi, dzina lake Abiyatara, adapulumuka, nathaŵa kutsatira Davide. Ndipo adauza Davide kuti Saulo adapha ansembe a Chauta. Davide adauza Abiyatara kuti “Ha! Tsiku limene lija nditaona kuti Doegi Mwedomu ali konkuja, ndidaadziŵa kuti kosapeneka konse akauza Saulo. Nchifukwa chake tsono uli pa ine mlandu wa imfa ya onse a m'banja la bambo wako. Koma iwe khala ndi ine, usaope ai, pakuti amene akufuna moyo wako, akufunanso moyo wanga. Ukakhala ndi ine, ukhala pabwino.” Tsiku lina Davide adamva kuti Afilisti akuthira nkhondo mzinda wa Keila, ndipo akufunkha zokolola za m'nkhokwe zao. Choncho Davide adafunsa Chauta kuti, “Kodi ndikamenyane nawo nkhondo Afilistiwo?” Chauta adamuuza kuti, “Pita, kamenyane nawo, kuti upulumutse mzinda wa Keila.” Koma Davide anthu ake adamuuza kuti, “Ngati tikuchita mantha ku Yuda konkuno, nanga nanji tikapita ku Keila kuti tikamenyane ndi magulu ankhondo a Afilisti? Kodi sitikaopa kwambiri kumeneko?” Tsono Davide adapemphanso nzeru kwa Chauta, ndipo adamuyankha kuti, “Nyamuka, upite ku Keila, pakuti ndidzaŵapereka Afilistiwo kwa iwe.” Tsono Davide ndi anthu ake aja adapita ku Keila, ndipo adakamenyana nawo Afilistiwo. Adapha ankhondo ambiri nalanda ng'ombe zao. Choncho Davide adapulumutsa anthu amene ankakhala ku Keila. Pamene Abiyatara, mwana wa Ahimeleki, adathaŵira kwa Davide ku Keila, adabwera atatenga efodi yaunsembe ija m'manja mwake. Saulo atamva kuti Davide wafika ku Keila, adati, “Mulungu wampereka m'manja mwanga. Pamene waloŵa mu mzinda umene uli ndi zipata ndi mipiringidzo yolimba, ndiye kuti wadzimanga yekha.” Tsono Saulo adasonkhanitsa ankhondo ake, naŵatuma ku Keila kuti akamzinge Davide pamodzi ndi anthu ake. Koma Davide adaadziŵa kuti Saulo akufuna kumchita chiwembu. Choncho adauza wansembe Abiyatara kuti abwere ndi efodi ija. Tsono Davide adalankhula ndi Mulungu kuti, “Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, ndithudi, ine mtumiki wanu ndamva kuti Saulo akufunafuna kubwera kuno ku Keila, kuti adzaononge mzindawu chifukwa cha ine. Kodi anthu a ku Keila adzandipereka kwa Saulo? Kodi Saulo adzabweradi monga m'mene ine mtumiki wanu ndamvera? Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, ndikukupemphani kuti mundiwuze, ine mtumiki wanu.” Chauta adati, “Saulo abweradi.” Tsono Davide adafunsanso kuti, “Kodi anthu a ku Keila adzandipereka ine ndi anthu anga kwa Saulo?” Chauta adati, “Inde adzakupereka.” Pamenepo Davide, pamodzi ndi ankhondo ake amene analipo ngati 600, adachokako ku Keila, namayenda chothaŵathaŵa. Saulo atamva kuti Davide wathaŵa ku Keila, adaleka zoŵatuma ankhondo aja. Davide ankabisala m'mapanga m'dziko lamapiri ku chipululu cha Zifi. Monsemo Saulo ankamufunafuna, koma Mulungu sadalole kuti agwidwe ai. Davide adaona kuti Saulo akumfunafuna kuti amuphe. Pa nthaŵiyo Davide anali ku chipululu cha Zifi ku Horesi. Tsono Yonatani, mwana wa Saulo, adanyamuka napita kwa Davide ku Horesi, ndipo adamlimbitsa mtima pomuuza kuti Mulungu adzamteteza. Yonatani adauza Davide kuti, “Usaope, abambo anga sadzakupha. Udzakhala mfumu ya Aisraele, ndipo ine ndidzakhala wachiŵiri kwa iwe. Abambo angawo akudziŵanso zimenezi.” Pamenepo aŵiriwo adachita chipangano pamaso pa Chauta. Choncho Davide adakhalabe ku Horesi, ndipo Yonatani adabwerera kwao. Tsono anthu a ku Zifi adapita kwa Saulo ku Gibea, nakamuuza kuti, “Davide akubisala ku dera lakwathu m'mapanga a ku Horesi pa phiri la Hakila limene lili kumwera kwa Yesimoni. Tsono inu amfumu, ife tadziŵa kuti mukumfunafuna kwambiri, choncho bwerani ndithu. Ifeyo tidzampereka kwa inu.” Apo Saulo adati, “Chauta akudalitseni, pakuti mwandikomera mtima. Pitani mukaonetsetse. Mukafufuze kumene kuli mbuto yake, ndi kupeza munthu amene wamuwona chamaso kumeneko. Ndikumva kuti ngwochenjera mwaukapsala. Nchifukwa chake muwone malo onse amene amabisalako, ndipo mubwerenso kuno kuti mudzandiwuze chenicheni. Tsono ndidzapita nanu. Ndipo ngati alidi kumeneko, ndidzamfunafuna pakati pa anthu onse m'dziko lonse la Yuda.” Anthuwo adabwerera ku Zifi, Saulo asananyamuke. Pa nthaŵiyo Davide ndi anthu ake anali ku chipululu cha Maoni ku Araba, kumwera kwa Yesimoni. Tsono Saulo ndi anthu ake adapita kukamfunafuna Davide, koma iye anali atazimva. Nchifukwa chake adathaŵa napita ku thanthwe la ku chipululu cha Maoni. Saulo atamva kuti Davide adathaŵira ku Maoni, adamlondola kuchipululu komweko. Saulo adadzera mbali ina ya phiri, Davide ndi anthu ake adadzeranso mbali ina ya phirilo. Tsono Davide ndi anthu ake adafulumira kuthaŵa, pamene Saulo ndi anthu ake anali pafupi kuŵagwira. Nthaŵi yomweyo padafika wamthenga amene adauza Saulo kuti, “Mufulumire kubwera, pakuti Afilisti akulithira nkhondo dzikoli.” Choncho Saulo adalekeza kulondola Davide, napita kukamenyana ndi Afilisti. Nchifukwa chake malo amenewo adaŵatchula Mwala wa malekano. Davide adachoka kumeneko, nakhala m'mapanga a ku Engedi. Saulo atabwerako kumene ankamenyana ndi Afilisti kuja, adamva kuti Davide ali ku chipululu cha Engedi. Tsono adatenga ankhondo okhoza zedi 3,000 amene adaŵasankha pakati pa ankhondo onse. Adapita kukafunafuna Davide ndi anthu ake ku Matanthwe a Mbalale. Adafika ku makola a nkhosa a pamphepete pa njira, pamene panali phanga. Saulo adaloŵa m'phangamo kuti akadzithandize. Pamenepo nkuti Davide ndi anthu ake akubisala m'kati mwenimweni mwa phangalo. Apo anthu a Davide aja adamuuza kuti, “Tsiku lija ndi lero limene Chauta ankanena, muja adaakuuzani kuti, ‘Ndidzapereka mdani wako m'manja mwako, udzamchita zomwe zidzakukomere.’ ” Tsono Davide adanyamuka, nakadulako chidutswa ku mkanjo wa Saulo, iyeyo osadziŵako ai. Koma pambuyo pake Davideyo adavutika mumtima mwake, chifukwa chakuti anali atadula chidutswa chija ku mkanjo wa Saulo. Tsono adauza anthu ake kuti, “Chauta andiletse kumchita choipa mbuyanga, wodzodzedwa wa Chauta. Ndisampweteke, popeza kuti ngwodzozedwa wa Chauta.” Choncho Davide atalankhula mau ameneŵa, anthu ake adamvera, pakuti sadaŵalole kuti amthire nkhondo Saulo. Pamenepo Saulo adatuluka m'phanga muja namapita. Pambuyo pake Davide nayenso adatuluka m'phangamo, ndipo adaitana Saulo kuti, “Mbuyanga mfumu.” Saulo atacheuka, Davide adamgwadira pogunditsa nkhope yake pansi. Adafunsa Saulo kuti, “Chifukwa chiyani mumamvera mau a anthu amene amanena kuti, ‘Davide akufuna kukuphani?’ Lero mwaonatu ndi maso anu kuti Chauta anakuperekani m'manja mwanga m'phanga muja. Ena ankandikakamiza kuti ndikupheni, koma ndakulekani dala. Ndinati, ‘Sindipweteka mbuyanga, poti ngwodzozedwa wa Chauta.’ Atate anga, onanitu chidutswa cha mkanjo wanu chili m'manja mwangachi. Pamenepo mudziŵe kuti mumtima mwanga mulibe cholakwa kapena zokuukirani, poti ndadula chidutswa ku mkanjo wanu, koma osakuphani. Sindidakulakwireni, ngakhale kuti inuyo mukufunafuna moyo wanga kuti mundiphe. Chauta aonetse kuti wolakwa ndani pakati pa ine ndi inu. Akulangeni chifukwa cha zimene mukundichitazi. Koma ine sindikupwetekani, ai. Paja anthu akale adati, ‘Munthu woipa, ntchito zake nzoipa.’ Motero ine sindikupwetekani, ai. Kodi mfumu ya Israele yadzalondola yani? Kodi ikufuna kugwira yani? Zedi, mukulondola ine galu wakufa! Mufuna kupha ine nthata! Nchifukwa chake Chauta aweruze, ndipo agamule pakati pa ine ndi inu kupeza wolakwa. Anditeteze. Aonetse kulungama kwanga pondipulumutsa kwa inu.” Davide atamaliza kulankhula mau ameneŵa, Saulo adafunsa kuti, “Kani liwu limeneli ndi lakodi, mwana wanga Davide?” Apo Saulo adayamba kulira mokweza. Adauza Davide kuti, “Iwe wachita chilungamo kupambana ine, pakuti wandichitira ine zabwino pamene ine ndakuchita zoipa. Lero waonetsa ubwino wako pakuti sudandiphe, Chauta atandipereka kwa iwe. Kodi munthu atapeza mdani wake, angalole kuti mdaniyo apulumuke? Motero Chauta akuchitire zabwino, chifukwa cha zimene wandichitira lerozi. Ona tsono, ndikudziŵa kuti udzakhala mfumu ndithu, ndipo kuti ufumu wa Israele udzakhazikika pa iwe. Undilonjeze molumbira tsono m'dzina la Chauta kuti sudzapha zidzukulu zanga ine nditamwalira, kuti dzina langa ndi la abambo anga lisaiŵalike.” Davide adalumbira zonsezi Saulo alikumva. Tsono Saulo adabwerera kwao, koma Davide ndi anthu ake adapitanso kuphanga kobisalira kuja. Samuele adamwalira. Ndipo Aisraele onse adasonkhana kudzalira maliro ake, namuika kumudzi kwao ku Lama. Masiku amenewo Davide adanyamuka, napita ku chipululu cha Parani. Tsono panali munthu wina ku Maoni amene anali ndi kadziko ku dera la mudzi wa Karimele. Munthuyo anali wolemera kwambiri. Anali ndi nkhosa 3,000 ndi mbuzi 1,000. Tsiku lina adayamba kumeta nkhosa zake ku Karimele. Munthuyo anali Nabala, wa fuko la Kalebe, ndipo mkazi wake anali Abigaile. Mkaziyo anali wanzeru ndi wokongola, koma mwamuna wakeyo anali wouma mtima ndi wankhanza. Anali wa fuko la Kalebe. Davide anali atamva kuchipululu kuja kuti Nabala akumeta nkhosa zake. Choncho adatuma anyamata khumi kuti, “Pitani ku phiri la Karimele kwa Nabala, mukandiperekere moni. Mukamulonjere motere: mukati mbuye wathu akuti, ‘Mtendere ukhale ndi inu ndi banja lanu ndi zinthu zonse zimene muli nazo. Ndikumva kuti muli ndi anthu ometa nkhosa. Pamene abusa anu anali nafe kuno, sitidaŵachite choipa chilichonse, ndipo sadasoŵe kanthu pa nthaŵi yonse pamene adakhala ku Karimele. Muŵafunse antchito anuwo, adzakuuzani. Nchifukwa chake muŵakomere mtima anyamata anga, pakuti tabwera nthaŵi ino yachikondwerero. Chonde muŵapatse anyamata angaŵa ndi ine bwenzi lanu Davide, chilichonse chimene mungakhale nacho.’ ” Tsono anyamata a Davide aja atafika, adafotokozera Nabala zonse zimene Davide adaaŵauza. Ndipo iwowo adayembekeza. Nabala adayankha anyamata a Davide aja poŵafunsa kuti, “Kodi Davide mwana wa Yese ndani? Ha! Masiku ano pali anthu antchito ambiri amene akuthaŵa kwa ambuyao. Kodi ndingatenge chakudya changa, madzi anga, nyama yanga imene ndaphera anyamata anga ometa nkhosa, kuti ndipatse anthu omwe sindikudziŵa kumene akuchokera?” Choncho anyamata a Davide adapotoloka, nabwerera kukauza Davide zonsezo. Apo Davide adauza ankhondo ake kuti, “Munthu aliyense amangirire lupanga lake.” Choncho aliyense adamangirira lupanga lake. Davide nayenso adamangirira lake. Anthu amene adapita ndi Davide analipo ngati 400. Koma anthu 200 adatsalira kuti azisunga katundu. Tsono wanchito wina adauza Abigaile, mkazi wa Nabala, kuti, “Davide adatuma amithenga kuchokera ku chipululu kuti adzalonjere mbuyathu, koma iwo adaŵakalipira. Komabe anthu amenewo adatichitira zabwino osati zoipa, poti sitidasoŵe kanthu nthaŵi zonse pamene tinali ndi iwowo ku busa. Ankatichinjiriza ngati linga usana ndi usiku, nthaŵi zonse pamene tinali ndi iwowo poŵeta nkhosa ku Rama. Tsono ndati mudziŵe zimenezi, ndipo muganizirepo zoti muchite, pakuti zimenezi zidzaonongetsa mbuyathu pamodzi ndi banja lao lonse. Chinanso nchakuti mbuyathu aja ndi a khalidwe lovuta, kotero kuti wina aliyense sangathe kulankhula nawo.” Tsono mwamsanga Abigaile adatenga mitanda yabuledi 200, matumba achikopa aŵiri a vinyo, nkhosa zisanu zootcheratu, makilogramu 17 a tirigu wokazinga, nchinchi za mphesa zoumika 100, ndiponso makeke ankhuyu 200. Zonsezo adazisenzetsa abulu. Kenaka adauza anyamata ake antchito kuti, “Batsogolani, ine ndikudza pambuyo panu.” Koma sadauze Nabala mwamuna wake. Tsono mkaziyo atakwera pa bulu ndi kufika patsinde pa phiri lina, adangoona Davide ndi ankhondo ake akubwera kwa iye. Ndipo mkaziyo adakumana nawo. Nthaŵiyo nkuti Davide atanena kuti, “Ndithudi ndidavutika pachabe kutchinjiriza zinthu zonse za munthu ameneyu, zimene anali nazo ku chipululu, kotero kuti palibe kanthu nkamodzi komwe pa zinthu zakezo kamene kadasoŵa. Koma iye wandibwezera zoipa m'malo mwa zabwino. Mulungu andilange ndithu ngati m'maŵa ndikhale nditasiyapo ngakhale munthu wamwamuna mmodzi mwa anthu onse amene ali nawo.” Abigaile ataona Davide, adatsika pa bulu msangamsanga, nadzigwetsa chafufumimba pamaso pake. Ali chigonere choncho ku mapazi a Davide adati, “Mbuyanga, mlandu ugwere ine ndekha basi. Chonde mulole mdzakazi wanune kuti ndilankhule nanu, ndipo mumve mau anga. Mbuyanga asasamale za amuna anga, munthu wa mkhalidwe wovuta uja. Monga momwe dzina lake liliri, iyenso ali choncho. Monga dzina lake limatanthauzira kuti chitsiru, zake zonse nzauchitsiru basi. Koma ine mdzakazi wanu, sindidaŵaone anyamata anu amene mudaaŵatumawo. Tsono mbuyanga, ndi Chauta yemwe amene wakuletsani kuti musaphe munthu ndi kulipsira ndi manja anu. Inu muli apa, pali Chauta wamoyo, ndikulonjeza molumbira kuti onse amene afuna kukuchitani choipa, adzalangidwa ngati Nabala. Pepani, nazi mphatsozi zimene mdzakazi wanune ndabwera nazo kwa inu mbuyanga, kuti zipatsidwe kwa anthu muli nawoŵa. Chonde, mukhululukire cholakwa cha ine mdzakazi wanu. Zoonadi, Chauta adzakhazikitsa banja lanu mu ufumu, poti mukummenyera nkhondo. Motero choipa sichidzapezeka mwa inu masiku onse a moyo wanu. Ngati anthu akuukirani namakulondolani kuti akupheni, Chauta Mulungu wanu adzakusungani, monga m'mene munthu amasungira chuma m'phukusi. Koma moyo wa adani anu, Iye adzautaya kutali, monga m'mene munthu amaponyera mwala ndi khwenengwe. Inu mbuyanga, Chauta adzakuchitirani zabwino zonse zimene adakulonjezani, ndipo adzakuikani kuti mukhale mfumu yolamulira Aisraele. Nthaŵi imeneyo inu simudzamva chisoni kapena kuvutika mu mtima kuti mudakhetsa magazi kapena kulipsira popanda chifukwa. Ndipo pamene Chauta adzakuchitirani zabwino zonsezi, musadzandiiŵale ine mdzakazi wanu.” Apo Davide adauza Abigaile kuti, “Inu mai, atamandike Chauta, Mulungu wa Israele, amene wakutumani kuti mukumane nane lero. Mulungu akudalitseni chifukwa cha nzeru zimene mwaonetsa lero pondiletsa kuti ndisakhetse magazi ndi kulipsira ndi manja anga. Chauta, Mulungu wa Israele, ndiye wandiletsa kuti ndisakupwetekeni. Zoonadi, pali Chauta, Mulungu wamoyo, mukadapanda kudzakumana nane msanga, ndithu sipakadamtsalira Nabala munthu wamwamuna ndi mmodzi yemwe maŵa m'maŵa.” Motero Davide adalandira kwa mkaziyo zimene adaamtengera, namuuza kuti, “Pitani kunyumba kwanu ndi mtendere. Mau anu ndaŵamva ndipo zopempha ndavomera.” Abigaile adabwerera kwa Nabala nampeza m'nyumba mwake akuchita phwando lalikulu ngati la mfumu. Nabala anali wosangalala mumtima mwakwe, poti anali ataledzera kwambiri. Tsono mkazi wakeyo sadamuuze kanthu kalikonse mpaka m'maŵa kutacha. M'maŵa mwake, m'maso mwa Nabala mutayera, mkazi wakeyo adamuuza zonse. Pomwepo Nabala mtima wake udaima, ndipo thupi lidangoti gwa ngati mwala. Patapita masiku khumi, Chauta adakantha Nabala naafa. Tsono Davide atamva kuti Nabala wafa, adati, “Atamandike Chauta amene walipsira chipongwe chimene adandichita Nabala, ndipo wandiletsa ine mtumiki wake kuti ndisachite choipa. Chauta wabwezera pamutu pa Nabala ntchito zake zoipa.” Tsono Davide adatuma anyamata ake kukafunsira mbeta Abigaile kuti akhale mkazi wake. Anyamata a Davide atafika kwa Abigaile ku Karimele, adamuuza kuti “Mfumu Davide watituma kuti tikutengeni, mukakhale mkazi wake.” Mkaziyo adagwada nagunditsa nkhope yake pansi, nati, “Ine mdzakazi wa mbuyanga Davide, ndili wokonzeka ngakhale kusambitsa mapazi a anyamata ake.” Motero Abigaile adanyamuka mofulumira nakwera pa bulu, ndipo pamodzi ndi anamwali ake asanu amene ankamtumikira, adatsata amithenga a Davide aja, nakakhala mkazi wake wa Davide. Davide anali atakwatira Ahinowamu wa ku Yezireele, ndipo aŵiri onsewo adakhala akazi ake. Paja Saulo anali atakwatitsa mwana wake Mikala, mkazi wa Davide, kwa Paliti mwana wa Laisi wa ku Galimu. Tsiku lina anthu a ku Zifi adabwera kwa Saulo ku Gibea, namuuza kuti, “Davide akubisala ku phiri la Hakila limene lili kuvuma kwa Yesimoni.” Saulo adanyamuka napita ku chipululu cha Zifi atatenga ankhondo 3,000 osankhidwa, kuti akafunefune Davide kuchipululuko. Adamanga zithando zankhondo pa phiri la Hakila, limene lili pambali pa mseu, chakuvuma kwa Yesimoni. Koma Davide adakhalabe kuchipululuko. Tsono ataona kuti Saulo akumlondola, Davide adatuma anthu oti akazonde, ndipo adapezadi kuti Saulo wafika. Ndiye Davide adanyamuka nakafika pa malo amene Saulo adaamangapo zithando zake. Ndipo adaona malo amene ankagonapo Sauloyo ndi Abinere mwana wa Nere, mkulu wa ankhondo a Saulo. Sauloyo ankagona m'zithandomo, ndipo gulu lonse lankhondo lidaamanga zithando pomzungulira. Tsono Davide adafunsa Ahimeleki Muhiti ndi Abisai mkulu wa Yowabu, mwana wa Zeruya, kuti, “Kodi ndani apite nane ku zithando za Saulo?” Abisai adati, “Ine ndipita nanu.” Choncho Davide ndi Abisai adakaloŵa ku zithando zankhondo usiku. Saulo anali gone m'chithando chake, atazika mkondo wake pansi cha kumutu kwake. Abinere ndi ankhondo onse adaagona momzungulira. Abisai adauza Davide kuti, “Mulungu wapereka mdani wanu kwa inu lero. Bwanji tsono mundilole kuti ndimbaye ndi mkondo kamodzinkamodzi ndi kumkhomerera pansi, sindichita kumbaya kaŵiri.” Koma Davide adamuuza kuti, “Ai, usamuphe. Ndani angathe kupweteka wodzozedwa wa Chauta nakhala wosachimwa?” Ndipo adalamulira kuti, “Pali Chauta wamoyo, Chautayo ndiye adzamkanthe kapena pamene lidzafike tsiku lake lakumwalira, kapena pamene adzapite ku nkhondo nakaphedwa. Chauta andiletse kuti ndisapweteke wodzodzedwa wake. Koma tsono tingotenga mkondo umene uli kumutu kwakewu ndi mtsuko wa madziwu, ndipo tizipita.” Motero Davide adatenga mkondo ndi mtsuko wa madzi, zimene zinali kumutu kwa Saulo, nachokapo. Palibe amene adaona zimenezo ngakhale kuzidziŵa, ndipo panalibe wina aliyense amene adadzuka. Onse anali m'tulo, chifukwa chakuti Chauta adaaŵagonetsa tulo tofa nato. Pambuyo pake Davide adakwerera mbali ina nakaimirira pamwamba pa phiri, pakati nkusiya mpata waukulu. Tsono Davide adaitana gulu lankhondo ndi Abinere mwana wa Nere, naŵafunsa kuti, “Kodi sukumva iwe Abinere?” Abinere adayankha kuti, “Kodi ndiwe yani ukuitana mfumuwe?” Davide adafunsa Abinere kuti, “Kodi sindiwe mwamuna? Ndani ali wofanafana nawe m'dziko la Israele? Nanga chifukwa chiyani sudamlonde mbuyako mfumu? Tsopano apa munthu wina anabwera kumeneko kuti adzaphe mbuyakoyo. Zimene wachitazi si zabwino ai. Pali Chauta wamoyo, nonsenu muyenera kuphedwa chifukwa simudalonde mbuye wanu, wodzozedwa wa Chauta. Uyang'ane kumene kuli mkondo wa mfumu ndi mtsuko wa madzi, zimene zinali kumutu kwake.” Saulo adazindikira liwu la Davide, ndipo adafunsa kuti, “Kodi liwu limeneli ndi lako, iwe mwana wanga Davide?” Davide adayankha kuti, “Inde, ndi liwu langadi, mbuyanga mfumu. Chifukwa chiyani mbuyanga mukundilondola ine mtumiki wanu? Kodi ndachita chiyani? Kodi tchimo langa nlotani? Nchifukwa chake tsono, mbuyanga mfumu, mumve mau a ine mtumiki wanu. Ngati ndi Chauta amene wautsa mtima wanu kuti mundiwukire, Chautayo apepesedwe ndi nsembe. Koma ngati ndi anthu, iwowo Chauta aŵatemberere, pakuti tsono andipirikitsa, kuti ndisakhale nao m'dziko la Chauta. Akuti, ‘Pita katumikire milungu ina.’ Ndiye inu tsono musalole kuti ndifere kutali ndi Chauta, pakuti mfumu ya Aisraele yatuluka kudzandifunafuna ine nthata, monga momwe amachitira munthu wosaka nkhwali ku thengo.” Tsono Saulo adati, “Ndachimwa. Bwerera, mwana wanga Davide, sindidzakuchitanso choipa, popeza kuti moyo wanga wauwona ngati wa mtengo wapatali. Ndithu ndachita zauchitsiru ndipo ndachimwa kwambiri.” Apo Davide adayankha kuti, “Suwu mkondo wanu, mfumu. Tumani mmodzi mwa ankhondowo adzatenge. Chauta amadalitsa munthu wokhulupirika ndi wochita zabwino. Chauta anakuperekani m'manja mwanga lero, koma sindidaphe munthu wodzozedwa ufumu. Monga ndakusungirani moyo wanu leromu, momwemonso Chauta ateteze moyo wanga, ndipo andipulumutse m'mavuto anga onse.” Apo Saulo adauza Davide kuti, “Mulungu akudalitse mwana wanga Davide. Udzachita zazikulu, ndipo pa zonsezo udzapambana.” Choncho Davide adachokapo, ndipo Saulo adabwerera kwao. Davide adaganiza mumtima mwake kuti, “Tsiku lina Saulo adzandipha. Palibe china chimene ndingachitepo, koma kuthaŵira ku dziko la Afilisti. Choncho Saulo adzaleka kumandifunafuna m'dziko la Aisraele, ndipo ndidzapulumuka kwa iye.” Tsono Davide adanyamuka, ndipo pamodzi ndi ankhondo 600 amene anali naye, adapita kwa Akisi, mwana wa Maoki, mfumu ya ku Gati. Adakhala ndi Akisi ku Gati, iyeyo pamodzi ndi anthu ake, aliyense ndi banja lake. Davide anali ndi akazi ake aŵiri, Ahinowamu wa ku Yezireele ndi Abigaile wa ku Karimele, mkazi wamasiye wa Nabala. Saulo atamva kuti Davide wathaŵira ku Gati, sadamfunefunenso. Pambuyo pake Davide adauza Akisi kuti, “Ngati ndapeza kuyanja pamaso panu, mundipatse malo pa mudzi wina m'dziko mwanu kuti ndizikhala kumeneko. Kodi ine mtumiki wanu ndizikhaliranji pamodzi ndi inu mu mzinda wanu waufumu?” Choncho tsiku limenelo Akisi adapatsa Davide mudzi wa Zikilagi. Nchifukwa chake mudzi wa Zikilagi ngwa mafumu a Yuda mpaka lero lino. Motero Davide adakhala ku dziko la Afilisti chaka chimodzi ndi miyezi inai. Tsono Davide ndi anthu amene anali naye ankapita kwa Agesuri, Agerizi, ndi Aamaleke nakaŵathira nkhondo onsewo. Mitundu imeneyi inali nzika za dzikolo kuyambira kale. Dziko lao linkafika ku Suri ndipo linkachita malire ndi dziko la Ejipito. Pa maulendo ake ankhondowo Davide ankapha anthu a m'dzikolo, osasiyapo wamoyo mwamuna kapena mkazi. Koma ankatenga nkhosa, ng'ombe, abulu, ngamila, ndi zovala, ndipo zonsezo ankabwerera nazo kwa Akisi. Akisi akafunsa kuti, “Kodi munakamenya nkhondo ndi yani lero?” Davide ankati, “Tinakamenya nkhondo kumwera kwa Yuda,” mwina ankati, “Ku dziko la Ayeramiyele,” mwina ankati, “Ku dziko la Akeni.” Davide sankasiya wamoyo, mwamuna kapena mkazi, kuwopa kuti wopulumukayo angakanene ku Gati kuti, “Davide adatichita zakutizakuti.” Davide ankachita choncho nthaŵi zonse pamene ankakhala ku dziko la Afilisti. Ndipo Akisi adamkhulupirira Davide namaganiza kuti, “Davide wadzisandutsa munthu woipa wodedwa ndi anthu ake omwe Aisraele. Nchifukwa chake adzakhala mtumiki wanga pa moyo wake wonse.” Nthaŵi ina Afilisti adasonkhanitsa magulu ao ankhondo, kuti amenyane ndi Aisraele. Tsono Akisi adauza Davide kuti, “Udziŵe kuti iwe ndi anthu ako muyenera kupita nane ku nkhondo.” Davide adayankha kuti, “Chabwino, mudzaona zimene ndichite ine mtumiki wanu.” Akisi adati, “Chabwino, ndidzakuika kuti ukhale mlonda wonditchinjiriza pa moyo wako wonse.” Nthaŵi imeneyi nkuti Samuele atafa, ndipo Aisraele atalira maliro ake, namuika ku mzinda wake ku Rama. Saulo anali atachotsa anthu onse olankhula ndi mizimu ndi anthu onse oombeza maula am'dzikomo. Tsono Afilisti adasonkhana nadzamanga zithando zao zankhondo ku Sunemu. Saulo nayenso adasonkhanitsa Aisraele, ndipo adamanga zithando ku Gilibowa. Saulo ataona gulu laankhondo la Afilisti, adayamba kuwopa ndi kunjenjemera kwambiri. Adapempha nzeru kwa Chauta, koma sadamuyankhe ngakhale podzera m'maloto, kapena mwa Urimu kapena mwa aneneri. Pamenepo Saulo adauza nduna zake kuti, “Mundifunire mkazi wolankhula ndi mizimu kuti ndipite kwa iyeyo, ndikapemphe nzeru.” Ndunazo zidamuuza kuti, “Ku Endori aliko mkazi wolankhula ndi mizimu.” Tsono Saulo adadzizimbaitsa, navala zovala zachilendo, napita. Pamodzi ndi anthu aŵiri adakafika kwa mkaziyo usiku. Ndipo adamuuza kuti, “Undifunsire zam'tsogolo kwa mizimu, makamaka undiitanire mzimu wa amene ndimtchule.” Mkaziyo adati, “Inutu mukudziŵa zimene adachita mfumu Saulo. Suja adachotsa m'dziko muno anthu olankhula ndi mizimu ndiponso oombeza? Chifukwa chiyani tsono mukunditchera msampha kuti mundiphe?” Koma Saulo adalonjeza mkaziyo molumbira nati, “Pali Chauta wamoyo, sudzalangidwa kaamba ka zimenezi.” Apo mkaziyo adafunsa kuti, “Kodi ndikuitanireni yani?” Saulo adati, “Itanire Samuele.” Pamene mkaziyo adaona Samuele, adakuwa kwambiri nati, “Chifukwa chiyani mwandinyenga? Ndinu mfumu Saulo!” Tsono mfumuyo idamuuza kuti, “Usaope. Kodi ukuwona chiyani?” Mkaziyo adati, “Ndikuwona mzimu ukutuluka pansi.” Saulo adafunsa mkaziyo kuti, “Kodi maonekedwe a mzimuwo ngotani?” Mkaziyo adati, “Imene ikutuluka ndi nkhalamba, yavala mkanjo.” Apo Saulo adadziŵa kuti ndi Samuele ameneyo, ndipo adapereka ulemu pakuŵerama ndi kugunditsa nkhope yake pansi. Pamenepo Samuele adafunsa Saulo kuti, “Chifukwa chiyani wandivuta ponditulutsa kuti ndibwere kuno?” Saulo adayankha kuti, “Ndavutika kwambiri, pakuti Afilisti abwera kudzandithira nkhondo, ndipo Mulungu wandifulatira osandiyankhanso, ngakhale podzera mwa aneneri, kapena m'maloto. Nchifukwa chake ndakuitanani kuti mundiwuze zomwe ndiyenera kuchita.” Samuele adati, “Chifukwa chiyani ukufuna ine tsopano, chikhalirecho Chauta wakufulatira kale ndipo wasanduka mdani wako? Chauta wakuchita zomwe adakuuza kudzera mwa ine. Wakulanda ufumu, waupereka kwa wina, kwa Davide. Chauta akuchita zimenezi lero, chifukwa chakuti sudamvere mau ake, ndipo sudaonongeretu Aamaleke ndi zinthu zao. Tsono adzakupereka iweyo pamodzi ndi Aisraele kwa Afilisti. Ndipo maŵa, iwe ndi ana ako, mudzabwera kuli ine kuno. Ndithudi, Chauta adzapereka gulu lankhondo la Aisraele kwa Afilisti.” Pompo Saulo adagwa pansi, kuchita kuti nyutu, ali wodzazidwa ndi mantha chifukwa cha mau a Samuele. Ndipo analibenso nyonga, poti sadadye kanthu tsiku lonse. Apo mkazi uja adasendera pafupi ndi Saulo, ndipo ataona kuti akuchita mantha, adamuuza kuti, “Taonani, mdzakazi wanune ndakumverani. Ine ndataya moyo wanga pomvera zimene munandiwuza. Nchifukwa chake tsono, inunso mumvere mau anga. Mundilole ndikuikireni kabuledi pang'ono, mudye kuti muwone nyonga zoyendera.” Saulo adakana nati, “Ine sindidya ai.” Koma nduna zake pamodzi ndi mkaziyo adamkakamiza, ndipo adaŵamvera. Choncho adadzuka pansi paja nakhala pa bedi. Mkaziyo anali ndi mwanawang'ombe wonenepa, ndipo adamupha mwachangu. Adatenga ufa naukanyanga, naphika buledi wosatupitsidwa. Tsono adadzapereka bulediyo kwa Saulo ndi nduna zake, ndipo onse adadya. Pambuyo pake adanyamuka, nachokapo usiku womwewo. Afilisti adasonkhanitsa magulu ao ankhondo ku Afeki. Nawonso Aisraele adamanga zithando zankhondo pa chitsime cha ku Yezireele. Pamene atsogoleri ankhondo a Afilisti ankatsogoza magulu ao a ankhondo mazana angapo ndiponso zikwi zingapo, Davide ndi ankhondo ake ankayenda pambuyo ndi Akisi. Pamenepo atsogoleri aja a Afilisti adafunsa kuti, “Kodi Ahebriŵa akuchita chiyani kuno?” Akisi adayankha kuti, “Uyutu ndi Davide, mtumiki wa Saulo mfumu ya Aisraele. Iye wakhala nane tsopano masiku ambiri kapena nditi zaka, chibwerere chake kuno sindidampeze cholakwa chilichonse mpaka lero lino.” Koma iwo adamkalipira Akisiyo namuuza kuti, “Mumbweze munthuyo kuti abwerere ku malo amene mudampatsa. Sadzapita nafe ku nkhondo, kuwopa kuti kunkhondoko angakasanduke mdani wathu. Nanga munthu ameneyu angathe kudziyanjanitsa bwanji ndi mbuyake? Iyeyu angathe kuchita zimenezi pakupha anthu athu ali panoŵa. Ameneyutu ndi Davide, yemwe uja ankamuvinira ndi kumuimbira kuti, “ ‘Saulo wapha zikwi inde, koma Davide wapha zikwi khumikhumi?’ ” Apo Akisi adaitana Davide namuuza kuti, “Pali Chauta wamoyo, iwe wakhala wokhulupirika kwa ine, ndipo kutumikira kwako m'magulu anga ankhondo kwandikomera kwambiri. Sindidakupeze cholakwa kuyambira tsiku limene udabwera kuno mpaka lero lino. Komabe atsogoleri enaŵa sakukufuna. Choncho ubwerere tsopano. Upite mwamtendere, kuwopa kuti atsogoleri a Afilisti angaipidwe nawe.” Davide adamufunsa kuti, “Kodi ndachita chiyani? Kodi mwapeza chiyani pa ine mtumiki wanu, kuyambira nthaŵi imene ndidayamba kukugwirirani ntchito mpaka tsopano lino? Nanga ndilekerenji kukamenyana nkhondo ndi adani anu, mbuyanga mfumu?” Akisi adayankha kuti, “Ndikudziŵa kuti ndiwe wosalakwa ndithu, monga mngelo wa Mulungu. Komabe atsogoleri ankhondo a Afilisti akunena kuti, ‘Davide asapite nafe ku nkhondo.’ Tsono udzuke m'mamaŵa, pamodzi ndi anthu ako amene udabwera nawo, munyamuke kukangocha.” Choncho Davide ndi anthu omwe anali naye adanyamuka m'mamaŵa nabwerera ku dziko la Afilisti. Koma Afilisti adakafika mpaka ku Yezireele. Patapita masiku aŵiri, Davide ndi anthu ake adafika ku Zikilagi. Tsono adapeza kuti Aamaleke anali atasakaza dera la kumwera kwa Yuda ndi kuthira nkhondo mzinda wa Zikilagi. Adagonjetsa mzindawo, nauthira moto. Adatenga akazi kuti akhale akapolo, pamodzi ndi onse amene anali m'menemo, aang'ono ndi aakulu omwe. Sadaphepo ndi mmodzi yemwe, koma adaŵatenga amoyo napita nawo. Davide ndi anthu ake atafika kumzindako adaupeza utapsa, ndipo akazi ao ndi ana anali atatengedwa ukapolo. Tsono Davide ndi anthu ake adalira mokweza, mpaka mphamvu zolirira zidaŵathera. Nawonso akazi a Davide anali atatengedwa ukapolo. Maina ao anali Ahinowamu wa ku Yezireele ndi Abigaile mkazi wamasiye wa Nabala wa ku Karimele. Davide adavutika koopsa, pakuti anthu ankakamba zoti amponye miyala, chifukwa cha chisoni chao pokumbukira ana ao aamuna ndi aakazi. Koma Davide adapeza mphamvu mwa Chauta, Mulungu wake. Pamenepo Davide adauza wansembe Abiyatara, mwana wa Ahimeleki, kuti, “Undipatse efodi ija.” Abiyatara adampatsa. Tsono Davide adapempha nzeru kwa Chauta nati, “Kodi ndilitsatire gulu lankhondo la Aamaleke? Kodi ndidzaŵapambana?” Chauta adamuyankha kuti, “Litsatire, pakuti udzalipambana ndithu ndipo udzaŵapulumutsa akapolowo.” Choncho Davide adanyamuka pamodzi ndi anthu 600 amene anali naye. Ndipo adakafika ku mtsinje wa Besori nasiyako anthu ena. Pamodzi ndi anthu 400 adapitirira kuŵalondola Aamalekewo, koma anthu 200 amene anali atatopa, adatsalira m'mbuyo, pakuti sadathe kuwoloka mtsinje wa Besori uja. Anthu amene anali ndi Davide, akuyenda m'njira, adapeza Mwejipito, nabwera naye kwa Davide. Tsono adampatsa buledi naadya. Adampatsanso madzi akumwa, chidutswa cha keke yankhuyu, ndi nchinchi ziŵiri za mphesa zoumika. Iyeyo atadya, moyo wake udatsitsimuka, pakuti sadaadya chakudya chilichonse, kapena kumwa madzi, masiku atatu athunthu. Davide adafunsa munthuyo kuti, “Kodi iwe ndiwe munthu wa yani? Ndipo ukuchokera kuti?” Munthuyo adati, “Ndine Mwejipito, kapolo wa Mwamaleke. Mbuyanga adandisiya masiku atatu apitaŵa poti ndinkadwala. Tinkathira nkhondo dera la kumwera kwa Yuda, ku maiko a Akereti, ndi dera la Akalebe. Mwakuti tidatentha mzinda wa Zikilagi.” Davide adamufunsa kuti, “Kodi ungandiperekeze ku gulu lankhondo limenelo?” Munthuyo adati, “Muyambe mwalumbira kwa Mulungu kuti simundipha kapena kundipereka kwa mbuyanga. Mukatero ndikuperekezani ku gulu lankhondo limenelo.” Choncho uja adaperekeza Davide kumeneko. Nthaŵi imeneyo Aamalekewo anali atamwazikana ponseponse. Analikudya, kumwa ndi kuvina, chifukwa cha zofunkha zimene adaatenga ku dziko la Afilisti ndi ku dziko la Yuda. Tsono Davide ndi anthu ake adaŵathira nkhondo namenyana nawo kuyambira mbandakucha mpaka madzulo. Sadapulumukepo Mwamaleke ndi mmodzi yemwe, kupatula anthu 400 amene adakwera pa ngamira, nathaŵa. Motero Davide adalanditsa zinthu zonse zimene adaatenga Aamaleke. Ndipo adapulumutsanso akazi ake aŵiri aja. Panalibe kanthu kalikonse kamene kadasoŵapo. Adalanditsa ana aamuna ndi ana aakazi, ndiponso chilichonse chimene chidaatengedwa. Adalanditsanso nkhosa zonse ndi ng'ombe zomwe. Ndipo anthu ankakusa zoŵetazo namati, “Izi ndi za Davide.” Pambuyo pake Davide adakafika kwa anthu 200 otopa kwambiri ndi osathanso kuyenda aja, amene adaaŵasiya ku mtsinje wa Besori. Iwo adanyamuka napita kukakumana ndi Davide ndi anthu amene anali naye aja. Davide adaŵayandikira naŵalonjera. Pamenepo anthu ena oipa mtima ndi opandapake a m'gulu la amene adaapita ndi Davide aja, adati, “Chifukwa chakuti sadapite nafe, sitiŵapatsako zofunkha zimene talanditsazi, kungopatula kuti aliyense atenge mkazi wake ndi ana ake, ndipo achoke.” Koma Davide adaŵauza kuti, “Musachite choncho, abale anga, ndi zinthu zimene Chauta watipatsa. Chautayo watisunga ndi kupereka m'manja mwathu gulu lankhondo limene lidabwera kudzamenyana nafe. Ndani angakuvomerezeni pa zimenezi? Munthu amene adapita ku nkhondo ndiponso munthu amene ankasunga katundu, onsewo ayenera kulandira zigawo zao mofanana.” Tsono Davide adagamula kuti njira imeneyi ikhale lamulo lokhazikika pakati pa Aisraele, kuyambira tsiku limenelo mpaka pano. Davide atafika ku Zikilagi, adapatulako zofunkha kusungira abwenzi ake, atsogoleri a ku Yuda, nauza aliyense kuti, “Nayi mphatso yanu yotapa pa zolanda kwa adani a Chauta.” Mphatsozo zidaperekedwa kwa anthu a ku Betele, a ku Ramoti kumwera kwa Yuda, a ku Yatiri, a ku Aroere, a ku Sifimoti, a ku Esitemowa, a ku Rakala, a ku mizinda ya fuko la Ayeramiyele, a ku mizinda ya fuko la Akeni, a ku Horoma, a ku Borasani, a ku Ataki a ku Hebroni ndiponso ku malo onse kumene Davide ankayenderako pamodzi ndi anthu ake. Afilisti adamenyananso nkhondo ndi Aisraele, ndipo Aisraelewo adathaŵa Afilisti, ndipo ambiri adakaphedwa ku phiri la Gilibowa. Afilistiwo adalondola Saulo ndi ana ake, ndipo adapha Yonatani, Abinadabu ndi Malikusuwa, ana a Saulo. Nkhondo idampanikiza kwambiri Sauloyo, ndipo anthu amauta adampeza namlasa koopsa. Pamenepo Saulo adauza wonyamula zida zake kuti, “Solola lupanga lako, undibaye, kuwopa kuti anthu osaumbalidwaŵa akabwera angadzandiseke ndi kundipha.” Koma wonyamula zida uja sadathe kuchita zimenezo, chifukwa ankachita mantha kwambiri. Ndiye Saulo adangotenga lupanga lake nagwerapo. Wonyamula zida uja ataona kuti Saulo wafa, nayenso adadzigwetsa pa lupanga lake nafera naye limodzi. Motero Saulo adafa pamodzi ndi ana ake atatu, kudzanso munthu wonyamula zida zake, kuphatikizapo ankhondo ake ambiri, onsewo tsikulo. Aisraele amene anali tsidya lina la chigwa cha Yezireele, ndiponso amene anali tsidya lina la Yordani, ataona kuti anzao adathaŵa, ndipo kuti Saulo ndi ana ake adafa, nawonso adathaŵa nasiya mizinda yao. Tsono Afilisti aja adabwera nkudzakhala m'menemo. M'maŵa mwake Afilisti atabwera kudzafunkha za anthu ophedwawo, adapeza Saulo ataphedwa pamodzi ndi ana ake atatu pa phiri la Gilibowa. Adamdula mutu Sauloyo, namuvula zida zake zankhondo. Kenaka adatuma amithenga ku dziko lao lonse, kuti akafalitse uthenga wabwinowu kwa milungu yao ndi kwa anthu omwe. Tsono adaika zida zankhondo za Sauloyo m'nyumba yopembedzeramo Asitaroti, mulungu wao. Ndipo adakhomerera mtembo wake ku khoma la mzinda wa Betisani. Koma anthu a ku Yabesi-Giliyadi atamva zimene Afilisti adaamchita Saulo, amuna ena olimba mtima adanyamuka, ndipo adayenda usiku wonse, nakachotsa mtembo wa Saulo ndi mitembo ya ana ake ku khoma la Beteseani. Atabwerera ku Yabesi adatentha mitemboyo kumeneko. Pambuyo pake adatenga mafupa ao naŵakwirira patsinde pa mtengo wa mbwemba ku Yabesi, ndipo adasala zakudya masiku asanu ndi aŵiri. Saulo atamwalira, Davide adabwerako kumene adaakagonjetsa Aamaleke kuja, ndipo adakakhala ku Zikilagi masiku aŵiri. Tsono pa tsiku lachitatu lake, adangoona munthu akuchokera ku zithando zankhondo za Saulo, atavala zovala zong'ambika ndiponso atadzithira dothi kumutu. Munthuyo atafika kwa Davide, adadzigwetsa pansi, namlambira. Davide adamufunsa kuti, “Ukuchokera kuti?” Iye adayankha kuti, “Ndathaŵa ku zithando zankhondo za Aisraele.” Davide adamufunsanso kuti, “Zinthu zidayenda bwanji? Tandiwuza.” Iye adati, “Anthu athaŵa kunkhondoko, ndipo ambirinso aphedwa. Saulo ndi mwana wake Yonatani, nawonso aphedwa.” Apo Davide adamufunsa mnyamatayo kuti, “Iwe wadziŵa bwanji kuti Saulo ndi Yonatani nawonso adafa?” Mnyamata wodzanena uja adati, “Zidangochitika kuti ndinali pa phiri la Gilibowa. Kumeneko ndidaona Saulo atangoti zyoli ku mkondo wake. Nthaŵi imeneyo nkuti magaleta ankhondo, ndiponso adani okwera pa akavalo atamuyandikira Sauloyo. Tsono Saulo atacheuka nandiwona, adandiitana. Ndidavomera kuti, ‘Ŵaŵa.’ Adandifunsa kuti, ‘Ndiwe yani?’ Ine ndidati, ‘Ndine Mwamaleke.’ Apo adandiwuza kuti, ‘Bwera pafupi, undiphe, chifukwa ndikumva ululu woopsa, komabe ndikali moyo.’ Choncho ndidasendera pafupi, nkumupha, poti ndidaadziŵa kuti akagwa, sakhala moyo. Tsono ndidamuvula chisoti chaufumu kumutu kwake ndi chigwinjiri kumkono kwake, ndipo ndabwera nazo kuno kwa inu mbuyanga.” Apo Davide adang'amba zovala zake. Nawonso anthu amene anali naye adachita chimodzimodzi. Ndipo anthuwo adabuma maliro. Adalira ndi kusala zakudya mpaka madzulo chifukwa cha Saulo ndi Yonatani mwana wake. Adaliranso chifukwa cha Aisraele, anthu a Chauta, chifukwa choti anali ataphedwa ku nkhondo. Tsono Davide adafunsa mnyamata wodzanena uja kuti, “Kodi iwe ndiwe wa kuti?” Iye adati, “Munthune ndine mwana wa mlendo, Mwamaleke.” Davide adamufunsanso kuti, “Nanga iwe sudachite mantha bwanji kutambalitsa dzanja lako nkupha wodzozedwa wa Chauta?” Pomwepo Davide adaitana mmodzi mwa ankhondo ake, namuuza kuti, “Mtenge ameneyu, ukamuphe.” Wankhondoyo adamkanthadi naafa. Ndipo Davide adati, “Wadziphetsa wekha, unanena wekha ndi pakamwa pako kuti, ‘Ndidapha wodzozedwa wa Chauta.’ ” Choncho Davide adaimba nyimbo ya madandaulo, kulira Saulo ndi Yonatani mwana wake. Ndipo adalamula kuti mau a madandaulowo aŵaphunzitse kwa anthu a ku Yuda. Mau ake ndi aŵa, monga adalembedwera m'buku la Yasara. “Ulemerero wako wathera zitunda zako zachipembedzo, iwe Israele. Ha! Kani amphamvu agwa motere! Musakanene zimenezi ku Gati, musakalengeze m'miseu ya ku Asikeloni, kuti akazi a Afilisti angasekerere, akazi a anthu osaumbalidwa angakondwe. “Inu mapiri a ku Gilibowa, pa inu pasagwe mame ndi mvula, pa inu pasapezeke minda yobereka dzinthu. Paja kumeneko adani adanyoza chishango cha munthu wamphamvu, chishango cha Saulo, chosapukutidwapo ndi mafuta. “Uta wa Yonatani sudabwereko chabe osakhetsa magazi a anthu osabayako ankhondo amphamvu. Ndipo lupanga la Saulo silidabwereko chabe osapha anthu. “Saulo ndi Yonatani pa moyo wao anali okondedwa ndi okondwetsa, ndipo sadalekane ali moyo ngakhale pa imfa. Anali ndi liŵiro loposa la ziwombankhanga. Anali amphamvu kuposa mikango. “Inu akazi a ku Israele, mlireni Saulo. Chifukwa cha iye uja munkavala zovala zabwino zofiira, ndiponso munkaika zokometsera zagolide pa zovala zanu. “Ha! Kani amphamvu agwa motere! Yonatani ali gone, atafa pa zitunda zako zachipembedzo. “Mbale wanga Yonatani, ndikuvutika mu mtima chifukwa cha iwe, wakhala wapamtima wanga. Chikondi chako pa ine chinali chodabwitsa kwambiri, chinali choposa ngakhale chikondi cha akazi. “Ha! Kani amphamvu agwa motere, zida zao zankhondo nkuwonongeka!” Pambuyo pake, Davide adafunsa Chauta kuti, “Kodi ndipite kukakhazikika ku mzinda wina uliwonse wa ku Yuda?” Chauta adamuuza kuti, “Inde, pita.” Apo Davide adafunsa kuti, “Tsono ndipite kuti?” Chauta adati, “Pita ku Hebroni.” Motero Davide adapita kumeneko pamodzi ndi akazi ake aŵiri aja, Ahinowamu wa ku Yezireele, ndi Abigaile mkazi wamasiye uja wa Nabala wa ku Karimele. Ndipo Davide adabwera ndi anthu ake aja amene anali nawo, aliyense ndi banja lake. Adakhala m'midzi ya ku Hebroni. Tsono anthu a ku Yuda adafika, ndipo kumeneko adadzoza Davide kuti akhale mfumu yao. Davide atamva kuti ndi anthu a ku Yabesi-Giliyadi amene adaika Saulo m'manda, adatuma amithenga kwa anthuwo kukaŵauza kuti, “Chauta akudalitseni, poti mudaonetsa kukhulupirika kwanu pomuika Saulo mbuyanu. Tsopano Chauta akuwonetseni chikondi chake chosasinthika, ndiponso kukhulupirika kwake kwa inu. Ndipotu inenso ndidzakuchitirani zabwino chifukwa cha zimene mwachitazi. Nchifukwa chake tsono mulimbe mtima, ndipo muchite chamuna. Paja mbuyanu Saulo adamwalira, ndipo anthu a mtundu wa Yuda andidzoza ine kuti ndikhale mfumu yao.” Abinere mwana wa Nere, amene ankalamula ankhondo a Saulo, anali atatenga Isiboseti mwana wa Saulo, kupita naye kutsidya, ku Mahanaimu. Tsono adamlonga ufumu kuti akhale mfumu ya Giliyadi, Asere, Yezireele, Efuremu ndi Benjamini, kungoti Israele yense. Isiboseti, mwana wa Saulo, anali wa zaka 40 pamene adayamba kulamulira Israele, ndipo ufumu wake udakhala zaka ziŵiri. Koma fuko la Yuda lidatsata Davide. Ndipo Davide adakhala mfumu ya fuko la Yuda ku Hebroni zaka zisanu ndi ziŵiri ndi theka. Tsono Abinere mwana wa Nere pamodzi ndi ankhondo a Isiboseti mwana wa Saulo adapita ku Gibiyoni kuchokera ku Mahanaimu. Yowabu mwana wa Zeruya pamodzi ndi ankhondo a Davide adapita kukakumana nawo ku dziŵe la Gibiyoni. Adakhala pansi, ena tsidya lina la dziŵelo, enanso tsidya lina. Abinere adauza Yowabu kuti, “Anyamata anu ndi athu abwere, amenyane tiwone.” Yowabu adati, “Chabwino, namenyane.” Anyamatawo adabweradi naŵaŵerenga. A fuko la Benjamini, anyamata a Isiboseti, mwana wa Saulo, analipo khumi ndi aŵiri, anyamata a Davide analinso khumi ndi aŵiri. Tsono aliyense adagwira mutu wa mnzake nabaya mnzakeyo m'nthitimu ndi lupanga. Choncho onse 24 adafera limodzi. Nchifukwa chake malo amenewo adaŵatchula kuti Helikati-Hazurimu, ndipo ali ku Gibiyoni. Tsono panali nkhondo yoopsa tsiku limenelo. Abinere pamodzi ndi anthu a ku Israele adagonjetsedwa ndi ankhondo a Davide. Yowabu, Abisai ndi Asahele, ana atatu aja a Zeruya, anali komweko. Asahele anali waliŵiro ngati insa. Iyeyo adathamangitsa Abinere. Pothamangapo sankayang'ana uku ndi uku, maso anali pa Abinere basi. Tsono Abinere adacheuka nati, “Kodi ndiwe, Asahele?” Iye adayankha kuti, “Ndine amene.” Abinere adamuuza kuti, “Patukira mbali ina iliyonse, ukagwire mmodzi mwa ankhondowo, umlande zake.” Koma Asahele sadafune kuti aleke kuthamangitsa Abinere. Tsono Abinere adauzanso Asahele kuti, “Iwe leke, usandithamangitse, bwanji ukundikakamiza kuti ndikuphe? Nanga ndikakupha, mbale wako Yowabu ndikaonana naye bwanji?” Koma Asahele sadafune kumleka. Choncho Abinere adabaya Asaheleyo m'mimba ndi luti la mkondo wake, mkondowo nkutulukira kumsana. Asahele adagwa pansi, kufa nkukhala komweko. Anthu onse amene adafika pamalo pomwe padafera Asahele, adangoima kungoti kakasi. Koma Yowabu ndi Abisai adayamba kuthamangitsa Abinere. Ndipo pamene dzuŵa linkaloŵa, adakafika ku phiri la Ama limene lili cha kuno kwa Giya, pa njira yopita ku chipululu cha Gibiyoni. Abenjamini adasonkhana pamodzi kuthandiza Abinere, ndipo adapanga gulu limodzi lankhondo, nakaima pamwamba pa phiri. Tsono Abinere adafuulira Yowabu namufunsa kuti, “Kodi tipitirirebe kumenyana mpakampaka? Monga sukudziŵa kuti mathero ake adzakhala oŵaŵa? Kodi udzaŵaletsa liti anthu ako kutithamangitsa ife abale ao?” Yowabu adayankha kuti, “Ndithudi, ndikulumbira, pali Mulungu wamoyo, ukadapanda kulankhula, ankhondo angaŵa sakadaleka kuŵathamangitsa abale aowo mpaka maŵa m'maŵa.” Choncho Yowabu adaliza lipenga, ndipo anthu onse adaleka, osathamangitsanso Aisraele, ndipo sadamenyane nawonso. Choncho Abinere ndi anthu ake adayenda usiku wonse, nabzola chidikha cha Araba. Adaoloka mtsinje wa Yordani, ndipo adayenda m'maŵa monse, nakafika ku Mahanaimu. Yowabu adabwerako kumene adaakathamangitsa Abinere kuja. Atasonkhanitsa anthu onse pamodzi, kudapezeka kuti padasoŵa ankhondo a Davide okwanira 19, pamodzi ndi Asahele. Koma ankhondo a Davidewo anali atapha anthu 360 a Abinere, a fuko la Benjamini. Tsono adatenga mtembo wa Asahele, nakauika m'manda a bambo wake, amene anali ku Betelehemu. Yowabu ndi anthu ake adayenda usiku wonse, ndipo kudaŵachera ali ku Hebroni. Kunali nkhondo nthaŵi yaitali pakati pa anthu a Saulo ndi anthu a Davide. Davide mphamvu zake zinkakulirakulira pamene anthu a Saulo ankafookerafookera. Davide adabereka ana aamuna ku Hebroni. Mwana wake woyamba anali Aminoni, wobadwa kwa Ahinowamu wa ku Yezireele. Wachiŵiri anali Kiliyabu, wobadwa kwa Abigaile, mkazi wamasiye wa Nabala, wa ku Karimele. Wachitatu anali Abisalomu, wobadwa kwa Maaka, mwana wa Talimai, mfumu ya ku Gesuri. Wachinai anali Adoniya, wobadwa kwa Hagiti. Wachisanu anali Sefatiya wobadwa kwa Abitala. Ndipo mwana wachisanu ndi chimodzi anali Itireamu, wobadwa kwa Egila. Ameneŵa ndiwo ana a Davide amene adabadwira ku Hebroni. Pamene kunali nkhondo pakati pa anthu a Saulo ndi anthu a Davide, Abinere adayamba kudzipatsa mphamvu pa anthu a Saulo. Saulo anali ndi mzikazi dzina lake Rizipa, mwana wa Aya. Tsono Isiboseti adafunsa Abinere kuti, “Chifukwa chiyani wakaloŵa kwa mzikazi wa bambo wanga?” Abinere adapsa nawo mtima kwambiri mau a Isiboseti, ndipo adati, “Kodi ukundiyesa ine galu wa Ayuda, adani athu? Kuyambira poyamba pomwe ndakhala wokhulupirika kwa Saulo bambo wako, abale ake, ndi abwenzi ake, ndipo sindidakupereke m'manja mwa Davide. Ndiye lero, iwe ukundiimba mlandu woti ndachimwa ndi mkazi! Nchifukwa chake Mulungu andilange, ngakhale kundipha kumene, ngati sindimchitira Davide zimene Chauta adamlonjeza. Ndidzachotsa ufumu pa banja la Saulo ndi kuupereka kwa Davide, kuti alamulire Israele ndi Yuda kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba.” Pamenepo Isiboseti adangoti kukamwa yasa, osatha kumuyankha Abinere mau ndi amodzi omwe, chifukwa ankamuwopa kwambiri. Tsono Abinere adatuma amithenga kwa Davide ku Hebroni kukamufunsa kuti, “Kodi dzikoli nlayani? Tipangane, ine ndidzakuthandizani kuti dziko la Israele likhale lanu.” Apo Davide adati, “Chabwino, tipangana. Koma ndikukupempha chinthu chimodzi: sudzandiwona ukapanda kubwera ndi Mikala, mwana wamkazi wa Saulo.” Tsono Davide adatuma amithenga kwa Isiboseti, mwana wa Saulo, kukanena kuti, “Undipatse mkazi wanga, Mikala, amene ndidamukwatira polipira timakungu 100 ta nsonga za mavalo a Afilisti.” Pamenepo Isiboseti adatuma anthu kuti akamtenge Mikalayo kwa mwamuna wake Palatiele, mwana wa Laisi. Koma mwamuna wakeyo adamtsatira mkaziyo. Mwamunayo ankapita nalira njira yonse mpaka ku Bahurimu. Abinere adamuuza kuti, “Iwe, bwerera.” Iye uja nkubwereradi. Pambuyo pake Abinere pokambirana ndi atsogoleri a Aisraele, adaŵauza kuti, “Nthaŵi yapitayi mwakhala mukufuna Davide kuti akhale mfumu yanu yokulamulani. Ndiye zimenezi muchitedi. Paja Chauta adalonjeza Davide kuti, ‘Ndidzapulumutsa anthu anga Aisraele kwa Afilisti kudzera mwa iwe mtumiki wanga, ndipo ndidzaŵapulumutsa kwa adani ao onse.’ ” Abinere adalankhulanso ndi anthu a fuko la Benjamini. Kenaka adakauzanso Davide ku Hebroni zonse zimene Abenjamini ndi Aisraele adavomerezana kuti achite. Pambuyo pake Abinere adabwera ndi anthu makumi aŵiri kwa Davide ku Hebroni. Davideyo adakonzera madyerero Abinere ndi anthu makumi aŵiri amene anali nawowo. Tsono Abinere adauza Davide kuti, “Loleni ndikasonkhanitse Aisraele onse kuti abwere kwa inu kuno, mbuyanga mfumu, kuti adzachite nanu chipangano, ndipo kuti muzilamulira kulikonse kumene mtima wanu ufuna.” Choncho Davide adamlola Abinere kuti apite. Ndipo iye adapita mwamtendere. Nthaŵi yomweyo ankhondo a Davide adafika ndi Yowabu kuchokera kumene adaakamenya nkhondo, atatenga zofunkha zambiri. Koma Abinere sanali ndi Davide ku Hebroni, popeza kuti anali atamlola kuti apite, ndipo iye anali atapitadi mwamtendere. Pamene Yowabu ndi ankhondo onse amene anali nawo adabwera, ena adauza Yowabuyo kuti, “Abinere mwana wa Nere adaabwera kwa amfumu, ndipo amfumuwo adamlola kuti apite, mwakuti wapitadi mwamtendere.” Atamva zimenezo Yowabu adapita kwa mfumu nakafunsa kuti, “Inu amfumu, kodi akuti mwachita zotani? Abinere wobwera bwinobwino kuno, nanga bwanjinso inu mwamlola kuti apite? Moti wapitadi? Inu amfumu, monga Abinere, mwana wa Nere, simumdziŵa? Amene ujatu adaabwera kudzangokumyatani m'maso. Adaafuna kudzangokutambwani, kuti adziŵe zonse zimene mukuchita.” Yowabu atachokako kwa Davide kuja, adatuma amithenga kuti amlondole Abinere. Iwowo adakampezadi ku chitsime cha Sira, nambweza, Davide osadziŵa kanthu. Pamene Abinere ankabwerera ku Hebroni, Yowabu adamtengera pambali, pafupi ndi chipata, nakhala ngati afuna kulankhula naye poduka mphepo. Pomwepo Yowabu adabaya Abinere m'mimba, nkuferatu. Yowabu adachita zimenezi chifukwa choti Abinere anali atamuphera mbale wake Asahele. Pambuyo pake Davide atamva, adati, “Ine pamodzi ndi anthu a mu ufumu wanga tilibe ndi mlandu womwe pamaso pa Chauta pa imfa ya Abinere, mwana wa Nere. Mlandu umenewu ugwere Yowabu ndi onse a pa banja la bambo wake. Ndipo Mulungu amlange Yowabuyu kuti pabanja pake pasadzakhale popanda munthu wa nthenda ya chidzonono, kapena wakhate, kapena wolumala, kapena wophedwa ku nkhondo kapenanso wosoŵa chakudya.” Choncho Yowabu ndi mbale wake Abisai adapha Abinere chifukwa choti Abinereyo anali ataŵaphera mbale wao Asahele pa nkhondo ya ku Gibiyoni. Tsono Davide adauza Yowabu ndi anthu onse amene anali naye kuti, “Ng'ambani zovala zanu, muvale ziguduli, kuti mulire maliro a Abinere.” Ndipo mfumu Davide mwiniwake ankatsatira onyamula mtembowo. Adakamuika Abinere ku Hebroni. Ndiye mfumu idalira mokweza mau ku manda a Abinere. Nawonso anthu onse adalira kwambiri. Polira maliro a Abinere mfumu Davide ankati, “Abinere nkufa motere, monga m'mene chimafera chitsiru? Manja ako anali osamanga, mapazi ako anali osakulunga. Komabe wafa monga m'mene amafera munthu m'manja mwa anthu oipa mtima.” Anthu onse adaliranso, kumlira Abinere. Kenaka anthuwo adadza kudzapempha mfumu kuti adye chakudya kudakali koyera. Koma Davide adalumbira kuti, “Mulungu andilange kwabasi, ngati ndidya chakudya kapena kanthu kena kalikonse dzuŵa lisanaloŵe.” Anthu onse adamvera zimenezo, ndipo zidaŵakomera. Zonse zimene ankachita mfumu zinkaŵakondwetsa anthu onse. Choncho onse amene ankakhala ndi mfumu pamodzi ndi Aisraele onse adamvetsa tsiku limenelo kuti sikunali kufuna kwa mfumu kuti Abinere mwana wa Nere aphedwe. Ndipo mfumu Davide adafunsa ankhondo ake kuti, “Kodi simukudziŵa kuti lero m'dziko la Israele mwagwa kalonga amene ali munthu wamkulu? Tsono ine lero ndafooka kwambiri, ngakhale kuti ndine mfumu yodzozedwa. Ndithu anthu ameneŵa, ana aamuna a Zeruya, akundivutitsa kwambiri. Chauta abwezere munthu wochita zoipa molingana ndi kuipa kwake.” Isiboseti, mwana wa Saulo, atamva kuti Abinere adakafera ku Hebroni, adataya mtima, ndipo Aisraele onse adachita mantha kwambiri. Isibosetiyo anali ndi anthu aŵiri amene anali atsogoleri a magulu ankhondo. Wina anali Baana, wina anali Rekabu, onsewo ana a Rimoni, wa fuko la Benjamini, wa ku Beeroti (pakuti Beeroti ndi chigawo cha Benjamini. Abeeroti adathaŵira ku Gitaimu, ndipo akhala akukhala nao kumeneko mpaka pano). Yonatani, mwana wa Saulo, anali ndi mwana wake wolumala miyendo, dzina lake Mefiboseti. Ndiye kuti mwanayo ali wa zaka zisanu, mbiri ya imfa ya Saulo ndi Yonatani idamveka ku Yezireele. Tsono mlezi wake wa mwanayo atamva, adamtenga mwana uja, nkuyamba kuthaŵa. Ndiye pothaŵa mofulumira choncho, mwanayo adampulumuka, nagwa pansi, nkuvulala. Kulumala kunali komweko. Tsono Rekabu ndi Baana, ana aja a Rimoni Mbeerotiŵa, adanyamuka. Masana dzuŵa likuswa mtengo, adakafika ku nyumba ya Isiboseti, nthaŵi imene iyeyo anali pa mpumulo wamasana. Mkazi wolonda pa khomo la nyumbayo ankapuntha tirigu, kenaka nkuyamba kuwodzera, nagona. Choncho Rekabu ndi Baana mbale wake adangoti kwakwalala kuloŵa. Aŵiriwo ataloŵa m'nyumbamo, adampeza Isibosetiyo ali gone pabedi pake. Iwo aja adambaya nkumupha, namdula mutu. Adanyamula mutuwo, nayenda nawo usiku wonse kudzera njira ya ku Araba. Tsono mutu wa Isibosetiwo adapita nawo kwa Davide ku Hebroni. Adauza mfumuyo kuti, “Amfumu, suwu mutu wa Isiboseti, mwana wa Saulo, mdani wanu uja ankafunafuna kukuphaniyu. Lero lino Chauta walipsirira Saulo ndi zidzukulu zake chifukwa cha inu mbuyanga.” Koma Davide adayankha Rekabu ndi Baana mbale wake kuti, “Ndithu pali Chauta wamoyo, amene waombola moyo wanga kwa adani anga onse, pamene wina adaandiwuza kuti Saulo wamwalira, naganiza kuti wabwera ndi uthenga wabwino, ine ndidamgwira, ndipo ndidamupha ku Zikilagi. Imeneyo idaali mphotho yomwe adalandira chifukwa cha uthenga wakewo. Nanga nanji anthu oipa amene adapha munthu wopanda chifukwa ali gone m'nyumba mwake, kodi ndingapande kukulangani chifukwa cha imfa ya munthuyo, mpaka kukuchotsani pa dziko lapansi?” Motero Davide adalamula ankhondo ake, ndipo adaŵapha anthuwo, naŵadula manja ndi mapazi, naŵapachika pambali pa dziŵe la ku Hebroni. Koma adatenga mutu wa Isiboseti, nakauika m'manda a Abinere ku Hebroni. Pambuyo pake mafuko onse a Aisraele adadzasonkhana kwa Davide ku Hebroni. Adamuuza kuti, “Ifetu ndi inuyo tili magazi amodzi. Kale Saulo adakali mfumu yathu yotilamulira, ndinuyo amene munkatsogolera Aisraele ku nkhondo nkubwera nawonso. Ndipo Chauta adaakuuzani kuti, ‘Udzakhala mbusa wa anthu anga Aisraele, udzakhala mfumu ya Israele.’ ” Choncho atsogoleri onse a Aisraele adadza kwa mfumu ku Hebroni. Tsono mfumu Davide adachita nawo chipangano pamaso pa Chauta ku Hebroniko, ndipo anthuwo adamdzoza Davideyo kuti akhale mfumu ya Aisraele onse. Davide anali wa zaka makumi atatu za kubadwa pamene adaloŵa ufumu. Adakhala mu ufumu zaka makumi anai. Ku Hebroni adalamulira Ayuda zaka zisanu ndi ziŵiri ndi theka. Ndipo ku Yerusalemu adalamulira Israele yense ndi Yuda zaka 33. Mfumu Davide ndi anthu ake adapita ku Yerusalemu kukamenyana ndi Ayebusi. Ayebusiwo anali nzika za dzikolo. Anthuwo adauza Davide kuti, “Sudzaloŵa muno ai. Anthu akhungu ndi anthu opunduka ndiwo adzakupirikitse.” Komabe Davide adalanda linga la Ziyoni, ndiye kuti Mzinda wa Davide. Tsono tsiku limenelo Davide adati, “Aliyense wofuna kuti akakanthe Ayebusi, ayenera kudzera m'ngalande ya madzi, kuti akaphe opunduka ndi akhunguwo amene mtima wanga umadana nawo.” Nchifukwa chake amanena kuti, “Akhungu ndi opunduka sadzaloŵa m'Nyumba ya Chauta.” Tsono Davide adakhala mu mzinda wamalinga uja nautchula dzina lakuti, “Mzinda wa Davide.” Ndipo adamanga mzinda kuzungulira deralo kuyambira ku malo komwe kale kunali chidikha, kuvuma kwa phiri mpaka m'kati mwake. Motero mphamvu za Davide zidanka zikulirakulira, chifukwa Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, anali naye. Hiramu, mfumu ya ku Tiro, adatuma amithenga kwa Davide, pamodzi ndi mitengo ya mkungudza, ndiponso amisiri a matabwa ndi ena odziŵa kumanga ndi miyala. Iwowo adadzamangira Davide nyumba yachifumu. Motero Davide adazindikira kuti Chauta wamkhazikitsa kuti akhale mfumu yolamulira Aisraele, ndiponso kuti wakweza ufumu wake chifukwa cha Aisraele, anthu ake. Tsono Davide atafika ku Yerusalemu kuchokera ku Hebroni, adakwatira akazi ena natenganso azikazi ena kumeneko. Tsono adabereka ana ambiri, aamuna ndi aakazi. Naŵa maina a ana a Davide amene adabadwira ku Yerusalemu: Samuwa, Sobabu, Natani, Solomoni, Ibara, Elisuwa, Nefegi, Yafiya, Elisama, Eliyada ndi Elifeleti. Afilisti atamva kuti Davide wadzozedwa kukhala mfumu yolamulira dziko la Aisraele, adapita kukamfunafuna. Koma Davide atamva zimenezo, adatsikira ku linga. Tsono Afilisti adabwera nakhala momwazikana m'chigwa cha Refaimu. Davide adafunsa kwa Chauta kuti, “Kodi ndipite kukamenyana nawo nkhondo Afilistiwo? Kodi mudzaŵapereka m'manja mwanga?” Chauta adamuuza kuti, “Inde, pita. Ndidzaŵaperekadi Afilistiwo m'manja mwako.” Pamenepo Davide adapita ku Baala-Perazimu, ndipo adagonjetsa Afilistiwo kumeneko. Tsono adati, “Ine ndikufika, Chauta waŵang'amba pakati adani anga ngati madzi a chigumula.” Nchifukwa chake malo amenewo amatchedwa kuti Baala-Perazimu. Afilisti adasiya mafano ao kumeneko, ndipo Davide ndi anthu ake adatenga mafanowo napita nawo kwao. Nthaŵi ina Afilisti adabweranso, nandanda m'chigwa chija cha Refaimu. Davide atafunsa Chauta, adamuyankha kuti, “Usakaŵathire nkhondo kumaso. Uŵadzere cha kumbuyo, uŵathire nkhondo pa malo oyang'anana ndi mitengo ya mkandankhuku ija. Tsono ukakamva phokoso pa nsonga za mitengo ya mkandankhukuyo, pamenepo ukakonzeke, chifukwa ndiye kuti Chauta wakutsogolera kuti ukakanthe gulu lankhondo la Afilistiwo.” Davide adachitadi monga momwe Chauta adaamlamulira, ndipo adagonjetsa Afilistiwo kuyambira ku Geba mpaka ku Gezere. Davide adasonkhanitsanso ankhondo okwanira 30,000, amene adaŵasankha pakati pa Aisraele. Adanyamuka, napita pamodzi ndi ankhondo onse amene anali naye kuchokera ku Baala wa ku Yuda kuti akatenge Bokosi lachipangano la Chauta. Bokosilo limadziwika ndi dzina la Chauta Wamphamvuzonse, amene amakhala pa akerubi ngati pa mpando waufumu. Anthuwo adatulutsa Bokosi lachipanganolo m'nyumba ya Abinadabu, imene inali pa phiri, nalinyamula pa ngolo yatsopano. Tsono Uza ndi Ahiyo, ana a Abinadabu, ndiwo ankayendetsa ngolo yatsopanoyo imene idaanyamula Bokosi lachipanganolo kuchoka nalo ku nyumba ya Abinadabu ija ku phiri. Ahiyo ankayenda patsogolo pa Bokosi. Tsono Davide pamodzi ndi Aisraele onse ankakondwerera kwambiri kulemekeza Chauta poimba ndi mphamvu zao zonse nyimbo ndi azeze, apangwe, tizing'wenyeng'wenye, maseche ndi ziwaya zamalipenga. Ndipo atafika pa malo opunthirapo tirigu ku Nakoni, ng'ombe zidaafuna kugwa, ndiye Uza nkutambalitsa dzanja kuti agwirire Bokosi la Mulungu lija, naligwiradi. Pamenepo Chauta adampsera mtima Uzayo, chifukwa sadasunge mwambo, ndipo Mulungu adamkantha, nafera pomwepo pafupi ndi Bokosi la Mulungulo. Tsono Davide adakhumudwa chifukwa chakuti Chauta adaakantha Uza. Ndipo mpaka pano malo amenewo amaŵatchula kuti Pereziuza. Davide adachita mantha ndi Chauta tsiku limenelo, ndipo adafunsa kuti, “Kodi Bokosi la Chautali lingafike bwanji kwathu?” Motero Davide sadafunenso kuti abwere nalo Bokosi la Chautalo kwao ku mzinda wake wa Davide, koma adalipatutsira ku nyumba ya Obededomu Mgiti. Choncho Bokosi lachipanganolo lidakhala miyezi itatu m'nyumba ya Obededomu wa ku Gati. Ndipo Chauta adadalitsa Obededomu ndi banja lake lonse. Tsono Davide adamva kuti Chauta wadalitsa banja la Obededomu ndi zinthu zonse zimene anali nazo, chifukwa cha Bokosi lachipangano. Choncho iye adapita kukatenga Bokosi lachipanganolo, kulichotsa m'nyumba ya Obededomu, napita nalo ku mzinda wake, akukondwera. Ndipo anthu amene ankanyamula Bokosi lachipanganolo ankati akayenda mapazi asanu ndi limodzi, Davide ankapereka nsembe ya ng'ombe yamphongo ndi mwanawang'ombe wonenepa. Davide atavala efodi yabafuta ankavina molemekeza Chauta ndi mphamvu zake zonse. Choncho iye pamodzi ndi Aisraele onse adabwera ndi Bokosi lachipangano akufuula ndi kuliza mbetete. Pamene Bokosi lachipangano linkaloŵa mu mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Saulo adasuzumira pa windo, naona mfumu Davide akulumphalumpha ndi kuvina molemekeza Chauta. Pamenepo mkaziyo adayamba kunyoza Davide mumtima mwake. Anthu adaloŵa nalo Bokosi lachipangano lija, nakalikhazika pamalo pake m'kati mwa hema limene Davide adaamangira Bokosilo. Tsono Davide adapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano kwa Chauta. Atatsiriza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjanozo, adadalitsa anthu m'dzina la Chauta Wamphamvuzonse. Kenaka adagaŵira Aisraele onsewo, amuna ndi akazi, aliyense mtanda wa buledi, nthuli yanyama, ndiponso keke ya mphesa zouma. Tsono anthu onse adachokapo, napita aliyense kunyumba kwake. Pamene Davide adabwerera kuti akadalitse banja lake, Mikala, mwana wa Saulo, adadzamchingamira nati, “Nkutero mfumu ya Aisraele kudzilemekeza kwake lero! Mpaka kuchita kudzivula pamaso pa adzakazi a antchito ake, monga m'mene amachitira munthu wamisala, opanda ndi manyazi omwe!” Davide adamuyankha kuti, “Ndachita zimenezi molemekeza Chauta, amene adandisankhula ine kupambana bambo wako, ndiponso kupambana banja lonse la bambo wako. Ndipo adandiika kuti ndikhale mfumu ya Aisraele, anthu a Chauta. Choncho ndidzasangalalabe ndi kulemekeza Chauta. Ndidzadzinyoza ndithu kupambana pamenepa. Kapena ndidzakhala wonyozeka m'maso mwako, koma m'maso mwa adzakazi amene ukunenawo, ndidzakhala wolemekezeka.” Tsono Mikala, mwana wa Saulo, adaferamo osamuwona mwana. Nthaŵi imene mfumu Davide anali atakhazikika m'nyumba mwake, Chauta adampumuza kwa adani ake onse omzungulira. Tsono adauza mneneri Natani kuti, “Ine ndikukhala m'nyumba yachifumu yomanga ndi mitengo ya mkungudza, koma Bokosi lachipangano la Chauta likukhala m'hema.” Natani adauza mfumu kuti, “Ai, chitani chilichonse chimene mukuganiza mumtima mwanu, poti Chauta ali nanu.” Koma usiku womwewo Chauta adauza Natani kuti, “Kamuuze mtumiki wanga Davide kuti Ine Chauta ndikuti, Kani wayesa udzandimangira ndiwe nyumba yoti ndizikhalamo? Ine sindidakhalepo m'nyumba chiyambire tsiku limene ndidatulutsa Aisraele ku Ejipito mpaka lero lino. Ndakhala ndikuyenda uku ndi uku ndipo mokhala mwanga munali m'hema. Konse kumene ndakhala ndikuyenda ndi Aisraele onse, kodi ndidaauzapo ndi mmodzi yemwe mwa aweruzi a Aisraele, amene ndidaŵalamula kuti azisunga anthu anga, kuti, bwanji sudandimangire nyumba ya mitengo ya mkungudza? Nchifukwa chake tsono mtumiki wanga Davide umuuze kuti, Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, ndidakutenga kubusa kumene unkaŵeta nkhosa kuja kuti udzakhale mfumu yolamulira anthu anga Aisraele. Ndidakhala nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndidagonjetsa adani ako onse, iweyo ukupenya. Tsono ndidzakumveketsa dzina lako kuti lidzafanefane ndi dzina la anthu otchuka a pa dziko lapansi. Ndipo ndidzaŵasankhira malo anthu anga Aisraele, ndi kuŵakhazika kumeneko kuti akhale ku malo aoao popanda kuvutikanso. Anthu achiwawa sadzaŵazunzanso monga momwe adaachitira kale lija, kuyambira nthaŵi imene ndidaaika aweruzi a anthu anga Aisraele. Choncho ndidakupumitsa kwa adani ako onse. Kuwonjezera pamenepo, Chauta akukuuza kuti, Ine Chauta ndidzakhazikitsa banja lako. Masiku ako atatha kuti ulondole makolo ako ku manda, ndidzakuutsira chiphukira pambuyo pako, mmodzi mwa ana obereka iweyo, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake kolimba. Iyeyo ndiye adzandimangire Nyumba yomveketsa dzina langa, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake kuti ukhale wamuyaya. Ine ndidzakhala bambo wake, iye adzakhala mwana wanga. Akamadzandichimwira, ndizidzamulanga monga m'mene bambo amalangira ana ake. Koma sindidzamchotsera chikondi changa chosasinthika, monga m'mene ndidaachitira ndi Saulo, amene ndidamkana, kuti uloŵe ufumu ndiwe. Tsono banja lako pamodzi ndi ufumu wako ndidzazikhazikitsa mpaka muyaya pamaso panga. Ndithudi, ufumu wako udzakhazikika osatha konse.” Natani adalankhula ndi Davide potsata mau onseŵa, ndiponso potsata zimene adaziwona m'masomphenyaŵa. Tsono mfumu Davide adaloŵa m'chihema chopembedzeramo Chauta. Adakhala pansi nayamba kupemphera, adati, “Inu Chauta Wamphamvuzonse, ine ndine yani, ndipo banja langa nchiyani, kuti Inu mwandifikitsa mpaka pamene ndiliripa? Komabe zonsezi zinali zazing'ono kwa Inu Chauta Wamphamvuzonse. Mudalankhulanso za banja la ine mtumiki wanu, kulilosera za nthaŵi yaikulu yam'tsogolo. Mwandionetsa mibadwo yam'tsogolo, Inu Ambuye Chauta. “Nanga ine ndingathe kunena chiyaninso kwa Inu? Paja mumandidziŵa mtumiki wanune, Inu Chauta Wamphamvuzonse. Mwachita zazikulu zonsezi chifukwa cha lonjezo lanu, ndiponso potsata zimene mtima wanu umafuna, kuti mtumiki wanune ndidziŵe. “Zoonadi, ndinu aakulu, Inu Chauta Wamphamvuzonse. Malinga ndi zimene tidamva ndi makutu athu, palibenso wina aliyense wonga Inu, ndipo palibe Mulungu wina koma Inu nokha. Kodi ndi mtundu uti pa dziko lapansi uli wofanafana ndi anthu anu Aisraele, amene Inu Mulungu mudaŵaombola ku Ejipito kuti akhale anthu anu? Mudatchuka kwambiri poŵachitira zinthu zazikulu ndi zoopsa, ndiponso popirikitsa mitundu ina ya anthu pamodzi ndi milungu yao, pamene ankafika anthu anu. Mudadzikhazikitsira anthu anu Aisraele kuti akhale anthu anuanu mpaka muyaya. Ndipo Inu Chauta mudakhala Mulungu wao. “Tsopano Inu, Chauta Mulungu, musunge mpaka muyaya lonjezo lanu limene mudaachita ponena za ine mtumiki wanu ndi za banja langa. Muchite monga momwe mudaanenera. Choncho dzina lanu lidzalemekezedwa mpaka muyaya. Anthu azidzati, ‘Chauta Wamphamvuzonse ndi Mulungu wolamulira Aisraele.’ Tsono banja la ine Davide, mtumiki wanu, lidzakhazikika mpaka muyaya. “Inu, Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Aisraele, mwandiwululira ine mtumiki wanu kuti mudzakhazikitsa banja langa. Nchifukwa chake ine mtumiki wanu ndalimba mtima kuti ndinene pemphero limeneli kwa inu. Ndipo tsopano Inu Chauta Wamphamvuzonse, ndinu Mulungu, ndipo mau anu ngoona. Mwalonjeza kuti mudzandichitira zabwino zotere ine mtumiki wanu. Tsono ndikukupemphani kuti mudalitse mokondwa banja la ine mtumiki wanu, likhalebe pamaso panu mpaka muyaya. Pakuti mwatero ndinu Ambuye Chauta, choncho banja la mtumiki wanune lidzadalitsidwadi mpaka muyaya.” Pambuyo pake Davide adathira nkhondo Afilisti, naŵagonjetsa, ndipo adaŵalanda mzinda wa Metegama. Kenaka Davide adagonjetsa Amowabu. Adalamula onsewo kuti agone pansi m'mizere itatu pa gulu lililonse. Pagulu lililonse anali kupha anthu amene anali pa mizere iŵiri yoyamba, kusiyapo a mzere wachitatu. Choncho Amowabu adasanduka akapolo a Davide, nayamba kukhoma msonkho kwa iye. Davide adagonjetsanso Hadadezere, mwana wa Rehobu, mfumu ya ku Zoba, pamene Hadadezereyo ankapita kumtunda kwa mtsinje wa Yufurate, kuti akakhazikitsenso ulamuliro wake ku deralo. Davide adagwira ankhondo a Hadadezere. Okwera pa akavalo analipo 1,700, a pansi analipo 20,000. Ndipo adadula mitsempha ya miyendo ya akavalo onse okakoka magaleta, koma adasungako ena a magaleta 100. Pamene Asiriya a ku Damasiko adaabwera kudzathandiza Hadadezere, mfumu ya ku Zoba, Davide adapha anthu a ku Siriyawo okwanira 22,000. Pambuyo pake Davide adaika maboma a ankhondo ku Damasiko, m'dziko la Siriya. Choncho Asiriyawo adasanduka otumikira Davide, nayamba kukhoma msonkho kwa iye. Motero Chauta adampambanitsa Davideyo kulikonse kumene ankapita. Davide adatenga zishango zagolide zimene anyamata a Hadadezere ankanyamula, nabwera nazo ku Yerusalemu. Kuchokera ku Beta ndi ku Berotai, mizinda ya Hadadezere, Mfumu Davide adabwerako ndi mkuŵa wambiri. Pamene Toi mfumu ya ku Hamati adamva kuti Davide wagonjetsa gulu lonse lankhondo la Hadadezere, adatuma mwana wake Yoramu kwa mfumu Davide, kuti akamlonjere. Adaafunanso kukamuyamika chifukwa chakuti adaamenya nkhondo ndi Hadadezere namgonjetsa. Adaatero pakuti Hadadezereyo ankamenyana nkhondo ndi Toi kaŵirikaŵiri. Tsono Yoramuyo adabwera ndi mphatso zopangidwa ndi siliva, golide, ndi mkuŵa. Zimenezonso mfumu Davide adazipereka kwa Chauta pamodzi ndi siliva ndi golide amene adaafunkha kwa anthu a mitundu ina amene adaŵagonjetsa. Anthuwo anali Aedomu, Amowabu, Aamoni, Afilisti ndi Aamaleke. Zina zinali zimene adaafunkha kwa Hadadezere mwana wa Rehobu, mfumu ya ku Zoba. Mbiri ya Davide idamveka ponseponse. Pamene ankabwerera, anali atapha Aedomu 18,000 ku chigwa cha Mchere. Tsono adaika zigono za ankhondo pena ndi pena m'dziko la Edomu. Mu Edomu monse munali timagulu ta ankhondo, choncho Aedomu onse adasanduka otumikira Davide. Motero Chauta adampambanitsa Davide kulikonse kumene ankapita. Motero Davide adalamulira dziko lonse la Israele, ndipo ankayendetsa zonse mwachilungamo ndi mosakondera. Tsono Yowabu, mwana wa Zeruya, anali mtsogoleri wa ankhondo, ndipo Yehosafati, mwana wa Ahiludi, anali mlembi wolemba mbiri. Zadoki, mwana wa Ahitubi, ndiponso Ahimeleki, mwana wa Abiyatara, anali ansembe, ndipo Seraya anali mlembi. Benaya, mwana wa Yehoyada, anali nduna yoyang'anira Akereti ndi Apeleti, ndipo ana a Davide anali ansembe. Tsiku lina Davide adafunsa kuti, “Kodi alipo wina aliyense wa banja la Saulo amene adatsalako? Ndikufuna kuti ndimchitire chifundo chifukwa cha Yonatani.” Panali mtumiki wina wa banja la Saulo, dzina lake Ziba. Ameneyo adamuitana kuti apite kwa Davide. Tsono mfumu idamufunsa kuti, “Kodi iwe ndiwe Ziba?” Iye adayankha kuti, “Ndine amene, mtumiki wanu.” Apo mfumu idamufunsa kuti, “Kodi palibe wina aliyense wa pa banja la Saulo amene adatsalako? Ndikufuna kuti ndimchitire chifundo monga momwe ndidalonjezera kwa Mulungu?” Ziba adayankha kuti, “Padakali mwana wamwamuna wa Yonatani. Iyeyo ngwopunduka miyendo.” Mfumu idamufunsa kuti, “Ali kuti?” Ziba adayankha kuti, “Ali ku nyumba ya Makiri, mwana wa Amiyele, ku Lodebara.” Pamenepo mfumu Davide adatuma anthu kuti akamtenge, ndipo iwo adakamtengadi ku nyumba ya Makiri mwana wa Amiyele, ku Lodebara. Pamene Mefiboseti, mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, adafika kwa Davide, adaŵerama pamaso pake, napereka ulemu. Tsono Davide adati, “Mefiboseti!” Iyeyo adayankha kuti, “Ndabwera ine mtumiki wanu.” Davide adamuuza kuti, “Usaope. Ndifuna kukuchitira chifundo chifukwa cha Yonatani bambo wako, ndipo ndidzakubwezera dera lonse la Saulo mbuyako. Udzadya nane pamodzi masiku onse.” Iyeyo adamuŵeramira, nati, “Kodi ine mtumiki wanu ndine yani, kuti musamale galu wakufa ngati ine?” Tsono mfumu idaitana Ziba mtumiki wa Saulo, nimuuza kuti, “Zinthu zonse zimene zidaali za Saulo ndi zonse za pa banja pake ndazipereka kwa mwana wa mbuyako Saulo. Tsono iwe, ana ako ndi atumiki ako, muzidzamlimira iyeyo, ndi kumabwera ndi zinthu zokolola zakumunda, kuti banja la mbuyako likhale ndi chakudya. Koma Mefiboseti adzadya ndi ine masiku onse.” Ziba anali ndi ana aamuna 15 ndi atumiki 20. Tsono adauza mfumu kuti, “Mtumiki wanune ndidzachita zonse potsata zimene inu mbuyanga mfumu mwalamula.” Choncho Mefiboseti ankadya ndi Davide ngati mmodzi mwa ana a mfumu. Mefiboseti anali ndi mwana wamng'ono, dzina lake Mika. Ndipo anthu onse amene ankakhala m'nyumba ya Ziba, adasanduka atumiki a Mefiboseti. Choncho Mefibosetiyo adakhala ku Yerusalemu, poti iyeyo ankadya ku nyumba ya mfumu masiku onse. Koma tsono anali wolumala mapazi onse aŵiri. Pambuyo pake Nahasi mfumu ya Aamoni adamwalira, ndipo Hanuni mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Tsono Davide adati, “Ndidzakhala naye mokhulupirika Hanuni, mwana wa Nahasi, monga momwe bambo wake adaandichitira zabwino.” Motero Davide adatuma atumiki kuti akampepese Hanuni chifukwa cha imfa ya bambo wake. Tsono atumiki a Davidewo adakafika m'dziko la Aamoni. Koma akalonga a Aamoni adafunsa Hanuni mbuyawo kuti, “Kodi mukuganiza kuti m'mene Davide wakutumizirani anthu odzakupepesanimu, ndiye kuti akuchitira bambo wanu ulemu? Osati Davide watuma atumiki akewo kwa inu kuti adzafufuze ndi kuzonda mzindawu, ndipo kuti akauwona, auwononge?” Choncho Hanuni adagwira atumiki a Davide aja, naŵameta ndevu mwachiperengedzu. Kenaka adaŵadulira zovala zao pakati mpaka m'chiwuno, naŵabweza kwao. Tsono Davide adamva zimenezo, adatuma anthu kuti akaŵachingamire, chifukwa iwowo anali ndi manyazi kwambiri. Ndipo mfumu idati, “Mukaŵauze kuti abakhala ku Yeriko mpaka ndevu zitamera, pambuyo pake ndiye adzabwere kuno.” Tsono Aamoni atazindikira kuti adziputira mkwiyo wa Davide, adatuma anthu kukalemba ntchito Asiriya a ku Beterehobu ndi a ku Zoba, ankhondo apansi okwanira 20,000. Adalembanso mfumu ya ku Maaka ndi anthu ake okwanira 1,000, ndiponso anthu a ku Tobu okwanira 12,000. Davide atamva zimenezo, adatuma Yowabu ndi gulu lake lonse la ankhondo, amphamvu okhaokha. Pamenepo Aamoni adatuluka nandanda pa mizere yankhondo pa khomo la chipata cha mzinda. Koma Asiriya a ku Zoba ndi a ku Rehobu, ndiponso anthu a ku Tobu ndi a ku Maaka, anali paokha ku malo opanda mitengo. Yowabu ataona kuti nkhondo yamkhalira kumaso ndi kumbuyo komwe, adasankhula ankhondo amphamvu pakati pa Aisraele, naŵandanditsa moyang'anana ndi Asiriyawo. Anthu ena onse otsala adaŵaika m'manja mwa Abisai, mbale wake, ndipo adaŵandanditsa moyang'anana ndi Aamoni. Tsono Yowabu adauza Abisai kuti, “Ngati Asiriya andipose mphamvu, iweyo udzandithandize. Koma ngati Aamoni akupose mphamvu, ndiye kuti ineyo ndidzabwera kudzakuthandiza. Limba mtima, ndipo tichite chamuna chifukwa cha anthu athu, ndiponso chifukwa cha mizinda ya Mulungu wathu. Chauta achite zimene zimkomere.” Choncho Yowabu ndi anthu ake adasendera pafupi ndi Asiriya aja kuti amenyane nawo nkhondo, koma Asiriyawo adathaŵa iye akufika. Tsono Aamoni ataona kuti Asiriya athaŵa, nawonso adathaŵa pofika Abisai, nakaloŵa mu mzinda. Apo Yowabu adaleka kumenyana ndi Aamoni, nabwerera ku Yerusalemu. Koma Asiriya ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraele, adasonkanitsa ankhondo ao onse. Hadadezere mfumu yao adatuma amithenga kuti akabwere nawo Asiriya anzao amene anali patsidya pa mtsinje wa Yufurate. Ndipo adafika nawo ku Helamu pamodzi ndi Sobaki, mtsogoleri wa ankhondo wa Hadadezere. Davide atamva zimenezi, adasonkhanitsa ankhondo onse a Aisraele, naoloka mtsinje wa Yordani, nakafika ku Helamu. Apo Asiriya adandanda kuti alimbane ndi Davide, ndipo adamenyana nayedi. Koma pambuyo pake Asiriyawo adathaŵa, kuthaŵa Aisraele. Pamenepo Davide adapha anthu apa magaleta okwanira 700, ndi ankhondo okwera pa akavalo okwanira 40,000. Adamvulaza kwambiri Sobaki, mtsogoleri wa gulu lao la ankhondo uja, kotero kuti adafera pomwepo. Tsono mafumu onse amene ankatumikira Hadadezere, ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraele, adapangana nawo za mtendere, ndipo adayamba kutumikira Aisraelewo. Motero Asiriya nawonso adaopa kumathandizanso Aamoniwo. Pa nyengo yophukira mitengo, nthaŵi imene mafumu ankakonda kukamenya nkhondo, Davide adatuma Yowabu ndi atsogoleri ake ndi ankhondo a Aisraele onse. Adaononga Aamoni, nazinga mzinda wa Raba ndi zithando zankhondo. Koma Davide adatsalira ku Yerusalemu. Zidangochitika kuti tsiku lina chakumadzulo, Davide adadzuka pabedi pake, namayenda pamwamba pa denga la nyumba yake yaufumu. Ali padengapo, adaona mkazi wina akusamba. Mkaziyo anali wokongola kwabasi. Pomwepo Davide adatuma munthu kuti akafunsitse za mkaziyo. Ndipo munthuyo adamuuza kuti, “Mkazi ujatu ndi Bateseba, mwana wa Eliyamu, mwamuna wake ndi Uriya Muhiti.” Apo Davide adatuma amithenga kuti akamtenge mkaziyo. Iwo adabwera naye kwa Davide, ndipo Davideyo adagona naye. Nthaŵi imeneyo nkuti mkaziyo atangomaliza kusamba. Pambuyo pake mkazi uja adabwerera kunyumba kwake. Kenaka ataona kuti waima, adatumiza mau kwa Davide kukamuuza kuti, “Inetu ndi mommuja, sindili bwino!” Atamva zimenezi Davide adatumiza mau kwa Yowabu kuti, “Umtumize Uriya, Muhiti uja, abwere kuno.” Yowabu adatumizadi Uriya kwa Davide. Uriya atabwera, Davide adamufunsa m'mene analiri Yowabu kunkhondoko, ndiponso m'mene analiri anthu, ndi m'menenso nkhondo inkayendera. Kenaka Davide adauza Uriya kuti, “Pita kunyumba kwako, ukapumuleko.” Uriya adatuluka ku nyumba ya mfumu, ndipo mfumu idatumiza mphatso kukapereka kwa Uriya. Koma Uriya adagona pakhomo pa nyumba ya mfumu pamodzi ndi antchito onse a mbuye wake, sadapite kunyumba kwake. Tsono anthu adamuuza Davide kuti, “Uriyatu sadapite kunyumba kwake.” Davideyo adafunsa Uriya kuti, “Kodi suja iwe wachokera ku ulendo? Nanga bwanji sudapite kunyumba kwako?” Uriya adauza Davide kuti, “Bokosi lachipangano likukhala m'zithando, kudzanso Aisraele ndi Ayuda. Ndipo mbuyanga Yowabu pamodzi ndi ankhondo a mfumu akugona panja pamtetete. Ndiye ine ndingapite kunyumba kwanga kuti ndizikadya ndi kumwa, ndi kumakakhala ndi mkazi wanga? Pali inu amene, ine sindingachite zimenezo.” Apo Davide adauza Uriya kuti, “Utandale pompano lero, maŵa ndikulola kuti uzipita.” Choncho Uriya adatandala ku Yerusalemu tsiku limenelo mpaka m'maŵa mwake. Davide adaitana Uriya, nadya naye ndipo adamwa kwambiri, kotero kuti Davide adamledzeretsa. Komabe madzulo Uriya adapita kukagona pogona pake, pamodzi ndi antchito a mfumu, osapita kunyumba kwake. M'maŵa mwake Davide adalembera Yowabu kalata, napatsira Uriya yemweyo kalatayo kuti akapereke. M'kalatamo adalembamo kuti, “Uriyayo umuike patsogolo penipeni pamene pakulimba nkhondo, ndipo umlekerere yekha kuti alasidwe ndi kuphedwa.” Choncho pamene Yowabu ankazinga mzindawo, adaika Uriya pamalo pamene ankaŵadziŵa kuti pali ankhondo amphamvu. Tsono ankhondo amumzindamo adatuluka nadzamenyana ndi Yowabu. Ndipo ena mwa ankhondo a Davide adaphedwa. Uriya, Muhiti uja, nayenso adaphedwa. Zitatero, Yowabu adatuma wamthenga kwa Davide kukamuuza zonse zimene zidachitika kunkhondoko. Adauza wamthengayo kuti, “Utatha kumuuza mfumu mbiri yonse ya nkhondo, tsono ngati mfumu ikapse mtima, nikakufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mudapita kufupi ndi mzinda kuti mukamenye nkhondo? Kodi simunkadziŵa kuti adzakulasani kuchokera m'kati mwa linga? Kodi Abimeleki mwana wa Gideoni adamupha ndani? Kodi adamupha si mkazi, pomkunkhunizira mwalawamphero kuchokera pa linga, kotero kuti adafera ku Tebezi? Chifukwa chiyani mudakafika pafupi ndi khoma?’ Pamenepo iweyo ukanene kuti, ‘Wankhondo wanu, Uriya Muhiti uja, nayenso adaphedwa.’ ” Wamthenga uja adapita, nakafika kwa Davide, nakamuuza zonse zimene Yowabu adamuuza kuti akanene. Adauza Davide kuti, “Adani athu adaatipambana, ndipo adaatuluka kukalimbana nafe ku thengo. Koma ife tidaŵabweza mpaka ku khomo lakuchipata. Tsono anthu oponya mivi ankalasa ankhondo anu kuchokera m'linga. Ndipo ankhondo ena mwa ankhondo a inu mfumu adaphedwa. Wankhondo wanu uja, Uriya Muhiti, nayenso adaphedwa.” Apo Davide adauza wamthenga uja kuti, “Kamuuze Yowabu kuti, ‘Zimenezi usavutike nazo, poti wakufa sadziŵika. Ulimbike polimbana ndi mzindawo, ndi kuugonjetsa.’ Choncho ukamlimbitse mtima Yowabuyo.” Pamene mkazi wa Uriya adamva kuti mwamuna wake Uriya adaphedwa, adalira, kulira mwamuna wake. Mkaziyo atatha kulira malirowo, Davide adatuma munthu nakamtenga, nkubwera naye kunyumba kwa mfumu, ndipo Davide adamukwatira. Mkaziyo adambalira mwana wamwamuna. Koma zimene adachita Davidezi zidaipira Chauta. Pambuyo pake Chauta adatuma mneneri Natani kwa Davide. Natani atafika kwa Davide, adamphera fanizo lakuti, “Mu mzinda wina munali anthu aŵiri, wina wolemera, wina wosauka. Wolemerayo anali ndi nkhosa zambiri ndi ng'ombenso zambiri. Koma wosauka uja analibe nkanthu komwe kupatula kankhosa kakakazi kamodzi, kamene adaagula. Ndipo adakaŵeta kankhosako, mpaka kukula kali ndi iyeyo pamodzi ndi ana ake. Kankadyako chakudya chake cha munthuyo, mpaka kumamwera m'chikho chake. Kankagona pakhundu pake pa munthuyo, ndipo kankakhala ngati mwana wake wamkazi. Tsiku lina kunyumba kwa munthu wolemera uja kudafika mlendo. Munthu uja sadafune kutengako imodzi mwa nkhosa zake kapena imodzi mwa ng'ombe zake, kuti aphere mlendo wakeyo. M'malo mwake adakatenga nkhosa ya munthu wosauka uja, naphera mlendo amene adaadzamuchezera uja.” Atamva za munthuyo, Davide adapsa mtima kwambiri. Adauza Natani kuti, “Pali Chauta wamoyo, munthu amene adachita zimeneziyu, ayenera kuphedwa basi. Ndipo pa mwanawankhosayo abwezere ena anai, chifukwa chochita zotere, ndiponso popeza kuti analibe chifundo.” Apo Natani adauza Davide kuti, “Munthuyotu ndinu amene. Chauta, Mulungu wa Israele, akunena kuti, ‘Ine ndidakudzoza kuti ukhale mfumu ya Aisraele, ndipo ndidakupulumutsa kwa Saulo. Ndidakupatsa banja la mbuyako, kudzanso akazi a mbuyako kuti akhale m'manja mwako, ndipo ndidakupatsanso mtundu wa Israele pamodzi ndi fuko la Yuda. Tsono zimenezi zikadakuchepera, ndikadakuwonjezera zina zambiri. Chifukwa chiyani tsono wanyoza mau a Chauta, nuchita choipa pamaso pake? Wapha Uriya Muhiti ndi lupanga, ndipo wakwatira mkazi wake. Wamuphetsa Uriyayo kudzera mwa Aamoni. Nchifukwa chake tsono nkhondo siidzachoka pabanja pako chifukwa wandinyoza Ine, ndipo wakwatira mkazi wa Uriya Muhiti. Tsono Ine Chauta ndikuti, ndithu ndidzakugwetsera tsoka pabanja pako pomwepo. Ndidzakuchotsera akazi ako, iweyo ukupenya, ndi kuŵapereka kwa mnzako wina, ndipo adzagona nawo akazi ako dzuŵa likuwomba mtengo. Iwe unkachita zimenezo m'seri, koma Ine ndidzazichita pamaso pa Aisraele onse, masana ndithu.’ ” Apo Davide adauza Natani kuti, “Ndidachimwira Chauta.” Natani adati, “Chauta wakukhululukirani machimo anu, simufa. Komabe, popeza kuti pochita zimenezi mwanyoza Chauta kotheratu, mwana amene akubalireniyo adzafa.” Pompo Natani adabwerera kunyumba kwake. Motero Chauta adalanga mwana amene mkazi wa Uriya adabalira Davide, ndipo adadwala kwambiri. Nchifukwa chake Davide adapempherera mwanayo kwa Mulungu. Adaleka kudya, nakaloŵa m'nyumba, nkukagona pansi usiku wonse. Akuluakulu a ku nyumba ya mfumu adadzaima pambali pake kuti amuutse. Koma iye adakana kuuka, ndipo sadadye nawo chakudya anthuwo. Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, mwanayo adamwalira. Atumiki a Davide adaopa kukamuuza kuti mwanayo wafa. Adati, “Pamene mwanayo anali moyo, tinkalankhula naye Davide, koma sankatimvera. Tsono tingathe kukamuuza bwanji lero kuti mwana wafa? Mwina nkudzipweteka.” Koma pamene Davide adaona kuti atumiki ake akunong'onezana, adadziŵa kuti mwana uja wafa. Choncho adafunsa atumiki ake aja kuti, “Kodi mwana uja watisiya?” Atumikiwo adati, “Inde, watisiyadi.” Apo Davide adadzuka pansi paja, ndipo adakasamba, nadzola mafuta, nkusintha zovala zake. Tsono adakaloŵa m'nyumba ya Chauta, nakapembedza. Pambuyo pake adapita kunyumba kwake, naitanitsa chakudya. Ndipo anthu atabwera nacho, iye adadya. Tsono atumiki ake aja adamufunsa kuti, “Tatifotokozerani, kodi zimene mwachitazi nzotani? Pamene mwana uja anali moyo, inu munkakana kudya. Koma pamene adamwalira, inu mudadzuka, nkuyamba kudya.” Davide adati, “Pamene mwanayo anali moyo, ndinkakana zakudya ndipo ndinkalira, poti ndinkati, ‘Sizidziŵika, mwina kapena Chauta nkundikomera mtima, kuti mwanayo akhale moyo?’ Koma tsopano mwanayo wafa. Nanga ndizikaniranjinso zakudya? Kodi ndingathe kumbwezanso? Ine ndidzapitadi kumene kuli iyeko, koma iyeyo sadzabwereranso kwa ine.” Tsono Davide adatonthoza mtima wa mkazi wake Bateseba, nakaloŵa kwa mkaziyo. Pambuyo pake mkazi uja adabala mwana wamwamuna, ndipo Davide adamutcha dzina lake Solomoni. Chauta adamkonda mwanayo, ndipo adatumiza mau kudzera mwa mneneri Natani kuti mwanayo dzina lake likhale Yedidiya, chifukwa Chauta adaamkonda. Nthaŵi imeneyo Yowabu ndi ankhondo a Aisraele ankathira nkhondo Raba, likulu la Aamoni, ndipo anali pafupi kuulanda. Adatuma amithenga kwa Davide kukamuuza kuti, “Ndauthira nkhondo mzinda wa Raba, ndipo ndalanda nkhokwe yake ya madzi. Tsono inu musonkhanitse ankhondo onse otsala, ndipo bwerani mudzauzinge ndi zithando mzindawo ndi kuulanda, kuwopa kuti ine ndikalanda mzindawo, ungamatchedwe dzina langa.” Choncho Davide adasonkhanitsa ankhondo ake onse, ndipo adapita ku Raba, nakauthira nkhondo mzindawo, nkuulanda. Tsono Davide adaivula chisoti kumutu mfumu ya Aamoni. Chisoticho chinkalemera makilogramu agolide, ndipo pa chisotipo panali mwala wamtengowapatali. Davide adachivala chisoticho, natenga zofunkha zochuluka mumzindamo. Adaŵatulutsa anthu amumzindamo, nakaŵagwiritsa ntchito ndi masowo ndi mapiki ndi nkhwangwa, ndi kuŵaumbitsa njerwa. Umu ndimo m'mene adachitira ndi mizinda yonse ya Aamoni. Pambuyo pake Davide adabwerera ku Yerusalemu pamodzi ndi ankhondo onse. Abisalomu mwana wa Davide, anali ndi mlongo wake wokongola, dzina lake Tamara. Aminoni, mwana wina wa Davide, ankakonda Tamara. Iye sankagona tulo chifukwa cha Tamara mlongo wake, mpaka kuchita kudwala. Tamarayo anali namwali wosadziŵa mwamuna, ndipo kunkaoneka kuti chinali chosatheka kuti Aminoniyo amchite chilichonse. Koma Aminoni anali ndi bwenzi lake, dzina lake Yonadabu, mwana wa Simea, mbale wake wa Davide. Yonadabuyo anali munthu wochenjera kwambiri. Tsiku lina Yonadabu adafunsa Aminoni kuti, “Kodi iwe, mwana wa mfumu, chifukwa chiyani umaoneka woonda m'maŵa masiku onse? Bwanji osandiwuza ine?” Aminoni adamuyankha kuti, “Ine ndikukonda Tamara, mlongo wa mkulu wanga Abisalomu.” Tsono Yonadabu adamuuza kuti, “Kagone pabedi pako, ndipo uchite ngati wadwala. Bambo wako akafika kuti adzakuwone, umuuze kuti, ‘Mloleni Tamara, mlongo wanga, abwere andikonzere chakudya kuti ndidye. Adzandikonzere chakudyacho konkuno, ine ndikupenya, kuti ndichiwone, ndipo ndidzadyere m'manja mwake.’ ” Choncho Aminoni adagona, nachita ngati wadwala. Mfumu itabwera kudzamuwona, Aminoniyo adauza mfumuyo kuti, “Chonde, mulole mlongo wanga Tamara abwere, kuti adzandiphikire chakudya ine ndikupenya, kuti ndidzadyere m'manja mwake.” Davide adatumiza mau kwa Tamara kuti, “Upite kunyumba kwa mbale wako Aminoni, ukamphikire chakudya.” Tamara adapitadi kunyumba kwa mbale wake Aminoni ku malo kumene ankagona. Adatenga ufa, naukanda, naumba makeke, Aminoniyo akupenya, ndipo adaphika makekewo. Tsono adatenga chiwaya, nakhuthula makekewo, iye akupenya, koma Aminoniyo adakana kudya. Ndipo Aminoni adati, “Uzani anthu onse achoke.” Choncho anthu onse adachoka. Tsono Aminoni adauza Tamara kuti, “Bwera nacho chakudya chija m'chipinda muno kuti ndidzadyere m'manja mwako.” Tamara adatenga makeke amene adaaphikawo, napita nawo kwa Aminoni, mbale wake, m'chipindamo. Koma atafika nacho chakudyacho pafupi ndi Aminoni kuti adye, Aminoni adamgwira Tamara, namuuza kuti, “Bwera ugone nane, iwe Tamara.” Koma Tamarayo adayankha kuti, “Iyai, mlongo wanga, usandikakamize. Zimenezi sizidachitikepo nkale lonse ku Israele. Usachite zauchitsiru zotere. Kodi ine sindidzachita manyazi poyenda pakati pa anthu? Ndipo iwe udzakhala mmodzi mwa zitsiru pakati pa Aisraele. Nchifukwa chake tsono, chonde, ndapota nawe, ulankhule ndi amfumu, poti iwowo sadzandikaniza kuti ndikwatiwe nawe.” Koma Aminoni sadamve zimene ankanena Tamarazo. Ndipo popeza kuti anali ndi mphamvu zoposa Tamara, Aminoniyo adamkakamiza Tamarayo nagona naye. Pambuyo pake Aminoni adayamba kudana naye kwabasi Tamarayo, kotero kuti chidani chake ndi Tamara chidakula kwambiri kuposa chikondi chimene adaamkonda nacho. Ndipo Aminoniyo adauza Tamara kuti, “Dzuka, kazipita.” Koma Tamarayo adati, “Iyai, mlongo wanga, kundipirikitsa chotere nkulakwa koposa zimene wandichitazi.” Koma Aminoni sadafune kumva zimene ankanena Tamarazo. Pomwepo Aminoniyo adaitana mnyamata amene ankamtumikira, namuuza kuti, “Mtulutse mkaziyu, achoke pano, ndisamuwonenso, ndipo upiringidze chitseko iyeyo akatuluka.” Nthaŵi imeneyo Tamara adaavala deresi lalitali, la manja aatali, monga momwe ankavalira ana achinamwali a mfumu, amene sadadziŵeko amuna. Tsono mnyamata wa Aminoni uja adatulutsa Tamara, napiringidza chitseko mkaziyo atatuluka. Ndipo Tamara adadzithira phulusa kumutu, nang'amba chovala chake chachitali chimene adaavala. Ndipo adagwirira manja kumutu, namapita akulira mokweza njira yonse. Apo Abisalomu, mlongo wa Tamarayo, adamufunsa kuti, “Monga Aminoni uja wakuchimwitsa? Komabe, iwe khala phee, mlongo wanga. Iye uja ndi mlongo wako. Zimenezi usavutike nazo.” Choncho Tamara ankakhala ngati wofedwa kunyumba kwa mlongo wake Abisalomu. Davide atazimva zimenezi, adapsa nazo mtima zedi. Koma Abisalomu sadanenepo kanthu kalikonse kabwino kapena koipa kwa Aminoni. Pakuti Abisalomuyo adaamuzonda kwambiri Aminoni chifukwa choti adaakakamiza Tamara mlongo wake kuchita naye zoipa. Patapita zaka ziŵiri zathunthu, Abisalomu anali ndi anthu ake ku ntchito yometa nkhosa ku Baala-Hazori pafupi ndi Efuremu. Tsono adaitana ana aamuna onse a mfumu kuti akakhaleko. Adapita kwa mfumu nati, “Amfumu, ine mtumiki wanu ndikukachita ntchito yometa nkhosa ndi anthu anga. Ndimati ngati nkotheka mudzakhale nafe inuyo amfumu pamodzi ndi atumiki anu.” Koma mfumu idauza Abisalomu kuti, “Iyai, mwana wanga, tisachite kupita tonse, tingakakuvutitse.” Adayesera muno ndi muno kumuumiriza, komabe Davide sadapite nao, m'malo mwake adangomdalitsa Abisalomuyo. Tsono Abisalomu adati, “Chabwino, ngati inu simupita, bwanji apite nao ndi mbale wanga Aminoniyu.” Apo mfumu idafunsa kuti, “Chifukwa chiyani ukufuna kuti iyeyu apite nao?” Koma Abisalomu adamkakamiza ndithu mpaka Davide adalola kuti Aminoni pamodzi ndi ana onse aamuna a mfumu apite nao. Tsono Abisalomu adalamula antchito ake kuti, “Muwonetsetse nthaŵi imene Aminoni akhale ataledzera ndi vinyo. Ndikakuuzani kuti, ‘Kanthani Aminoni!’ Pomwepo mumuphe. Musaope, nanga sindine ndakulamulani? Mulimbe mtima, ndipo muchite chamuna.” Choncho atumiki a Abisalomu adamchita Aminoni monga momwe adaaŵalamulira Abisalomu. Zitatero, ana onse aamuna a mfumu adadzambatuka, aliyense adakwera pa bulu wake, nathaŵa. Koma anthuwo akali m'njira, Davide adamva mphekesera zakuti Abisalomu wapha ana onse aamuna a mfumu, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene watsalako. Pompo mfumu idadzuka, ning'amba zovala zake, nkudzigwetsa pansi. Atumiki ake onse amene anali pafupi naye, nawonso adang'amba zovala zao. Koma Yonadabu, mwana wa Simea, mbale wa Davide, adati, “Mbuyanga, musaganize kuti ana onse a inu mfumu aphedwa, Aminoni yekha ndiye waphedwa. Zimenezi zachitika poti nzimene Abisalomu adaatsimikiziratu kale, kuyambira pa tsiku limene Aminoni adakakamiza Tamara, mlongo wa Abisalomu, kuchita naye zoipa. Nchifukwa chake tsono mbuyanga mfumu, musavutike ndi maganizo oti ana anu onse aamuna aphedwa. Aminoni yekha ndiye waphedwa.” Nthaŵi imeneyo nkuti Abisalomu atathaŵa. Tsono mlonda wapalinga poyang'ana, adangoona anthu ambiri akuchokera ku mseu wa Horonaimu, m'mbali mwa phiri. Atamva zimenezi Yonadabu adauza mfumu kuti, “Ana a mfumu abwera. Amfumu, monga momwe ndinakuuzirani muja, ndi m'mene zayendera.” Tsono atangomaliza kulankhula, adangoona ana a mfumu akubwera, ndipo anawo adayamba kubuma maliro. Pomwepo mfumuyo nayonso idalira kwambiri pamodzi ndi atumiki ake. Abisalomu adathaŵa ndithu napita kwa Talimai, mwana wa Amihudi, mfumu ya ku Gesuri. Ndipo Davide adalira maliro a mwana wake Aminoni nthaŵi yaitali. Abisalomu adakhala ku Gesuri zaka zitatu. Tsono mfumu Davide adagwidwa ndi chifundo chofuna kumlondola Abisalomuyo. Pamenepo nkuti Davideyo atatonthozedwa pa imfa ya Aminoni. Yowabu, mwana wa Zeruya, adaadziŵa kuti mtima wa mfumu uli pa Abisalomu. Tsono adatuma anthu ku Tekowa kukatengako mkazi wanzeru kumeneko. Adauza mkaziyo kuti, “Ukhale ngati mfedwa, uvale zovala zaumasiye. Usadzole mafuta, koma ukhale ngati mkazi amene wakhala akulira masiku ambiri. Ukatero upite kwa mfumu, ukalankhule nayo izi, izi.” Choncho Yowabu adauza mkaziyo mau oti akanene. Mkazi wa ku Tekowayo atafika kwa mfumu, adadzigwetsa pansi, nalambira mfumu, ndipo adati, “Pepani amfumu, thandizeni.” Mfumuyo idamufunsa kuti, “Chikukuvutani nchiyani, mai?” Mkaziyo adayankha kuti, “Ha! Munthune ndine mkazi wamasiye. Mwamuna wanga adafa. Ndiye ine mdzakazi wanu ndinali ndi ana aamuna aŵiri, anawo ankamenyana kuminda. Panalibe wina aliyense woti aŵaleretse, choncho wina adakantha mnzake mpaka kumupha. Tsono banja lonse landiwukira ine mdzakazi wanu, akunena kuti, ‘Utipatse mwana wako amene adapha mbale wake, kuti ife timuphe chifukwa cha mbale wake amene iye adaphayo.’ Motero anthuwo adzaononganso mloŵachuma. Anthuwo adzapha mwana wanga amene wanditsalira, ndipo dzina la mwamuna wanga silidzakumbukika, pakuti sipadzakhalanso mwana pa banja lathu.” Apo mfumu idauza mkazi uja kuti, “Mai, pitani kunyumba kwanu, ndichitapo kanthu ineyo pa nkhaniyi.” Mkazi wa ku Tekowa uja adauza mfumu kuti, “Inu amfumu, mlandu umenewu ugwere ine ndi banja la bambo wanga, inuyo mukhale osalakwa pamodzi ndi banja lanu lonse.” Apo mfumu idati, “Ngati wina aliyense akunenerani kanthu kena kalikonse, mubwere naye kwa ine, ndipo sadzakuvutitsaninso.” Tsono mkazi uja adanena kuti, “Chonde, amfumu mupemphe kwa Chauta Mulungu wanu, kuti wolipsira imfa ija asaphenso wina, kuti choncho mwana wanga asaonongeke.” Davide adati, “Pali Chauta wamoyo, mwana wanu sadzapwetekedwa mpang'ono pomwe.” Tsono mkaziyo adati, “Chonde, mulole kuti ine mdzakazi wanu ndilankhule mau ena kwa inu mbuyanga mfumu.” Mfumuyo idamuuza kuti, “Lankhulani, mai.” Apo mkazi uja adafunsa kuti, “Chifukwa chiyani nanga mwaganiza zoŵachita zinthu zotere anthu a Mulungu? Chifukwatu pochita zimenezi inu amfumu mwadziimba mlandu nokha, malinga nkuti simudaitanitse wopirikitsidwa uja kuti abwererenso kwao. Paja madzi akatayika saoleka, ndiye tonsefe tiyenera kufa ndithu. Koma Mulungu safuna kuti moyo wa munthu utayike, tsono amakonza njira yakuti wopirikitsidwa asakhale wotayikiratu chonse. Ndiye ine ndafika kuti ndidzalankhule ndi inu amfumu. Mwina mwake mungathe kudzachita zimene mdzakazi wanune ndikupempha. Ndimaganiza kuti inu amfumu mutazimva, mudzandipulumutsa kwa munthu amene afuna kundiwononga ine pamodzi ndi mwana wanga, potero nkutichotsa pa kadziko kathu kamene adatipatsa Mulungu. Choncho ine mdzakazi wanu ndidaaganiza kuti mau anu mbuyanga mfumu adzandipulumutsa, poti inu muli ngati mngelo wa Mulungu, podziŵa zabwino ndi zoipa. Chauta Mulungu wanu akhale nanu.” Apo mfumu idamuyankha mkaziyo kuti, “Musandibisire kanthu kalikonse pa zimene ndikufunseni.” Mkazi uja adati, “Ai ndithu, mbuyanga mfumu sindikubisirani.” Tsono mfumuyo idafunsa kuti, “Kodi zimenezi Yowabu sakuzidziŵa?” Mkaziyo adayankha kuti, “Pali inu nomwe, mbuyanga mfumu, palibe munthu amene angathe kupewa kuyankha chilichonse chimene inu mwafunsa. Kunena zoona, mtumiki wanu Yowabu ndiye amene adandiwuza kuti ndichite zimenezi. Iyeyo ndiye adandiwuza ine mdzakazi wanu mau onseŵa. Mtumiki wanu Yowabu adachita zimenezi kuti asinthe mayendedwe ake a zinthu. Koma inu mbuyanga muli ndi nzeru zonga za mngelo wa Mulungu, mutha kudziŵa zinthu zonse za pa dziko lapansi.” Pambuyo pake mfumu idauza Yowabu kuti, “Chabwino tsono, ndavomera kuti zimenezi zichitike. Pita, kamtenge mnyamata uja Abisalomu.” Yowabu adaŵerama pansi, adalambira mfumu, naithokoza. Tsono adati, “Tsopano ndadziŵa kuti inu mbuyanga mfumu mwandikomera mtima, chifukwa mwavomera pempho langali.” Choncho Yowabu adanyamuka, adapita ku Gesuri, nakatenga Abisalomu, nkubwera naye ku Yerusalemu. Komabe mfumu idati, “Akhale payekha m'nyumba yakeyake. Asabwere pamaso panga.” Motero Abisalomu adakhala pa yekha m'nyumba yakeyake, osafika pamaso pa mfumu. M'dziko lonse la Israele panalibe munthu wina aliyense wokongola ndi wochititsa kaso ngati Abisalomu. Kuyambira kumapazi mpaka kumutu analibe chilema chilichonse. Chaka chilichonse ankameta tsitsi lake, chifukwa linkamlemera kwambiri. Ankati akalimeta Abisalomuyo, naliyesa pa sikelo tsitsilo, linkalemera makilogramu aŵiri, potsata muyeso wa mfumu. Abisalomu anali ndi ana aamuna atatu, ndi mwana wamkazi mmodzi, dzina lake Tamara. Iyeyu anali mkazi wokongola. Choncho Abisalomu adakhala zaka ziŵiri zathunthu mu Yerusalemu, osaonekera kwa mfumu. Tsiku lina adatumiza mau kwa Yowabu opempha kuti amtume kwa mfumu. Koma Yowabu sadafike. Abisalomu adatumizanso mau kachiŵiri, koma Yowabu osafika ndithu. Pamenepo Abisalomu adauza atumiki ake kuti, “Munda wa Yowabu uli pafupi ndi wanga, ndipo ali ndi barele m'menemo. Pitani kautentheni.” Pompo atumiki a Abisalomu adapita kukautentha mundawo. Tsono Yowabu adanyamuka kupita kunyumba kwa Abisalomu, nakamufunsa kuti, “Bwanji atumiki ako atentha munda wanga?” Abisalomu adayankha kuti, “Taona, ine ndinkatumiza mau kwa iwe kuti ndidzakutume kwa mfumu kukaifunsa kuti chifukwa chiyani ndidachoka ku Gesuri kubwera kuno? Kunali kwabwino koposa kuti ine ndizikhalabe konkuja.” Abisalomu adapitirira nati, “Ndipite basi kwa mfumu. Ngati ndili ndi cholakwa, mfumuyo ikandiphe.” Apo Yowabu adapita kwa mfumu, nakakambira mfumuyo zimenezo. Tsono mfumu idaitana Abisalomu. Iye adabwera kwa mfumu, nadzigwetsa pansi pamaso pa mfumu. Ndipo mfumuyo idamlandira bwino pakumumpsompsona. Zitapita zimenezi, Abisalomu adadzipezera galeta lokokedwa ndi akavalo, napezanso anthu makumi asanu omamperekeza. Abisalomu ankadzuka m'mamaŵa, namaima pa njira ya ku chipata cha mzinda. Munthu wina aliyense akakhala ndi mlandu kuti apite kwa mfumu kukaweruzidwa, Abisalomu ankamuitana, namufunsa kuti, “Ukuchokera ku mzinda uti?” Akayankha kuti, “Mtumiki wanune, ndine wa fuko lakutilakuti, m'dziko la Israele,” Abisalomu ankamuuza kuti, “Taona, zimene ukunenazi nzabwino ndi zolungama. Koma mfumu sidaike munthu woti azimva madandaulo anu.” Ndipo ankapitirira kunena kuti, “Achikhala adaaika ine, kuti ndikhale woweruza m'dziko muno! Bwenzi munthu aliyense amene ali ndi mlandu, kapena vuto lina lililonse, atabwera kwa ine, ndipo ine ndikadamuweruza molungama munthuyo.” Choncho nthaŵi zonse munthu ankati akasendera pafupi kudzalambira Abisalomuyo, iye ankatambalitsa mkono, ndipo ankamgwira munthuyo namumpsompsona. Umu ndimo m'mene Abisalomu ankachitira ndi Aisraele onse amene ankabwera kwa mfumu kuti akaweruzidwe. Motero Abisalomu adaŵagwira mitima Aisraele. Patapita zaka zinai, Abisalomu adapempha mfumu kuti, “Chonde mundilole kuti ndipite ku Hebroni kuti ndikachite zimene ndidalumbira kwa Chauta. Nthaŵi imene ndinkakhala ku Gesuri ku Aramu, ndidachita lumbiro lakuti, ‘Chauta akadzandibwezeradi ku Yerusalemu, ndidzampembedza ku Hebroni.’ ” Apo mfumu idamuuza kuti, “Upite ndi mtendere.” Choncho Abisalomu adanyamuka napita ku Hebroni. Koma Abisalomu adatuma amithenga m'seri kwa mafuko onse a Aisraele kukanena kuti, “Malinga mukangomva kulira kwa lipenga, munene kuti, ‘Abisalomu ndiye mfumu ya ku Hebroni.’ ” Abisalomu popita, adatenga anthu okwanira 200 a ku Yerusalemu. Iwoŵa anali alendo oitanidwa chabe, mwakuti ankangopita osadziŵa chilichonse. Pamene Abisalomu ankapereka nsembe ku Hebroni, adatumiza mau kukaitana Ahitofele, mlangizi wa Davide wa ku mzinda wa Gilo. Motero chiwembucho chidakula kwambiri. Nawonso anthu otsatira Abisalomu adanka nachulukirachulukira. Tsiku lina wamthenga adafika kwa Davide kudzanena kuti, “Aisraele onse ali pambuyo pa Abisalomu.” Ndiye Davide adauza ankhondo ake amene anali naye ku Yerusalemu kuti, “Nyamukani, tiyeni tithaŵe kuti tingasoŵe mpata wothaŵira Abisalomu. Fulumirani, kuti angatipeze mwamsanga, ndipo angatithire nkhondo ndi kutipha tonse mumzinda muno.” Apo nduna za mfumu zija zidauza mfumu kuti, “Amfumu, ife ankhondo anu tili okonzeka kuchita chinthu chilichonse chimene inu mungachitsimikize kuchita.” Choncho mfumu idatuluka, nipita pamodzi ndi anthu onse a pabanja pake. Koma mfumuyo idasiya azikazi ake khumi kuti azisunga mudzi. Pamene mfumu idatuluka, anthu onse adaitsata. Onsewo adakaima pa nyumba yomalizira. Ankhondo ake onse adayamba kuyenda pamaso pa Davide, ndipo Akereti ndi Apeleti kudzanso Agiti okwanira 600 amene adamtsata kuchokera ku Gati, nawonso adayenda pamaso pa mfumu. Zitatero, mfumu idafunsa Itai Mgiti kuti, “Chifukwa chiyani ukupita nafe pamodzi? Bwerera, ukakhale ndi mfumu ija. Paja iwe ndiwe mlendo, ndiponso ndiwe munthu wothaŵa kwanu, motero bwerera. Iwe wangobwera dzulo. Ndiye ine ndikutenge lero, kuti uzinka nuyenda nane? Ine ndemwe sindikudziŵa kumene ndikupita. Bwerera ndi anthu akwanu, ndipo Chauta akukomere mtima ndi kukuchitira zabwino mwa kukhulupirika kwake.” Koma Itai adayankha mfumu kuti, “Pali Chauta wamoyo, ndiponso pali inu nomwe mbuyanga mfumu, kulikonse kumene inu mbuyanga mfumu mudzakhale, kaya mpa imfa kaya mpa moyo, ine mtumiki wanu ndidzakhalanso komweko.” Choncho Davide adauza Itai kuti, “Chabwino, tiye.” Motero Itai Mgiti uja adaoloka mtsinje wa Kidroni, pamodzi ndi anthu ake, akuluakulu ndi ang'onoang'ono omwe amene anali naye. Tsono anthu onse adayamba kulira mofuula pamene mfumu ndi otsatira ake ankapita. Choncho mfumuyo idaoloka mtsinjewo, ndipo anthu onse adamtsatira kupita ku chipululu. Ansembe, Abiyatara ndi Zadoki adapita nao pamodzi ndi Alevi onse, atanyamula Bokosi lachipangano la Chauta. Adatula pansi Bokosilo, mpaka anthu onse atatuluka mumzindamo. Pamenepo mfumu idauza Zadoki kuti, “Nyamulani Bokosi lachipangano la Chautali, mubwerere nalo mu mzinda. Chauta akandikomera mtima, adzandibweza kuti ndidzaliwonenso Bokosilo pamodzi ndi malo ake omwe. Koma akapanda kukondwera nane, chabwino, andichite zomwe zimkomere.” Ndipo mfumuyo idauzanso Zadoki wansembe uja kuti, “Bwerera ku mzinda mwamtendere, iwe pamodzi ndi Abiyatara, ndi ana anu aŵiri, mwana wako Ahimaazi ndi Yonatani mwana wa Abiyatara. Tsono ine ndidzadikira ku madooko a Yordani ku chipululu mpaka nditalandira mau ochokera kwa inu ondiwuza m'mene ziliri zinthu.” Pamenepo Zadoki ndi Abiyatara adanyamula Bokosi lija nabwerera nalo ku Yerusalemu, ndipo adakakhala kumeneko. Koma Davide adakwera phiri la Olivi, akunka nalira, osavala kanthu kuphazi, atafundira kumutu. Anthu onse amene anali naye adafundanso kumutu, ndipo nawonso adakwera phiri akunka nalira. Kenaka Davide adamva kuti Ahitofele ali pakati pa anthu ogalukira, pamodzi ndi Abisalomu. Tsono Davideyo adayamba kupemphera, adati, “Ine Chauta ndikukupemphani, musandutse uphungu wa Ahitofele kuti ukhale uchitsiru.” Davide atafika pamwamba pa phiri pomwe ankapembedzerapo Mulungu, Husai Mwariki adadzakumana naye atang'amba mwinjiro ndi kudzithira dothi kumutu. Davide adamuuza kuti, “Ukapita nane, sizindithandiza kwenikweni. Koma makamaka iwe ubwerere ku mzinda, ukamuuze Abisalomu kuti, ‘Inu amfumu, ine ndidzakhala mtumiki wanu. Monga kale ndinali mtumiki wa bambo wanu, momwemonso tsopano ndidzakhala mtumiki wanu.’ Ukakatero ukandigonjetsera uphungu wa Ahitofele. Kodi Zadoki ndi Abiyatara si ansembe amene ali nawe kumeneko? Tsono chilichonse chimene ungachimve kunyumba kwa mfumu, ukaŵauze ansembe amenewo. Ahimaazi, mwana wa Zadoki ndiponso Yonatani, mwana wa Abiyatara, nawonso ali komweko. Ndipo podzera mwa iwowo udzandiwuza zonse zimene udzamve.” Choncho Husai, bwenzi la Davide, adaloŵa mu mzinda, nthaŵi yomwe Abisalomu ankaloŵa mu Yerusalemu. Davide atabzola pang'ono pamwamba pa phiri, adakumana ndi Ziba, mtumiki wa Mefiboseti, ali ndi abulu a chishalo pa msana, atasenza buledi wokwanira 200, masangwe a mphesa 100, zipatso zapachilimwe 100, ndiponso thumba la vinyo. Mfumu idafunsa Ziba kuti, “Chifukwa chiyani wabwera ndi zimenezi?” Ziba adayankha kuti, “Amfumu, abuluŵa ndi oti anthu a m'banja mwanu azikwerapo. Bulediyu, ndi zipatso zapachilimwezi nzoti ankhondo azidya, ndipo thumba la vinyoli nloti anthu amene azikomoka m'chipululu azimwa.” Kenaka mfumu idamufunsa kuti, “Nanga mwana wa mbuyako ali kuti?” Ziba adayankha kuti, “Watsalira ku Yerusalemu, poti akunena kuti, ‘Aisraele andibwezera ufumu wa bambo wanga tsopano.’ ” Apo mfumu idauza Ziba kuti, “Zonse zimene zinali za Mefiboseti nzako.” Ziba adati, “Pepani, ndakupembani, mbuyanga mfumu, bwanji nthaŵi zonse ndizipeza kuyanja pamaso panu!” Pamene mfumu Davide adafika ku mzinda wa Bahurimu, kudatulukira munthu wa ku banja la Saulo, dzina lake Simei, mwana wa Gera. Ankabwera akungotukwana. Simeiyo ankaponya miyala mfumu Davide ndiponso nduna zake zonse. Nthaŵiyo nkuti atetezi ake ndi ankhondo ake ali kwete kuzungulira mfumuyo. Simei potukwanapo ankati, “Choka, choka, iwe munthu wopha anthu, munthu wachabechabe. Chauta wakulipsira chifukwa chakuti udapha onse a banja la Saulo, nulanda ufumu wake. Ndipotu Chauta wapereka ufumuwo kwa mwana wako Abisalomu. Ona, kutha kwako nkumeneku, pakuti iweyo ndiwe wopha anthu.” Pamenepo Abisai, mwana wa Zeruya, adafunsa mfumu kuti, “Bwanji mukulola galu wakufayu kuti akutukwaneni chotere, inu mbuyanga mfumu? Mundilole ndikamdule pa khosi.” Koma mfumu idayankha kuti, “Zikukukhudzani bwanji zimenezi, inu ana a Zeruya? Ngati iyeyu akunditukwana chifukwa choti Chauta wachita kumuuza kuti, ‘Mtukwane Davideyu’, ndani angamufunse kuti, ‘Bwanji wachita zimenezi?’ Tsono Davide adauza Abisai ndi atsogoleri ake kuti, ‘Mwana wanga weniweni akufuna kundipha, nanga nanji Mbenjaminiyu? Mlekeni azitukwana, pakuti wachita kumlamula ndi Chauta kuti atero. Mwina mwake Chauta adzaona mavuto anga, nadzandibwezera zabwino chifukwa cha kunditukwanaku.’ ” Motero Davide ndi anthu ake ankayenda mu mseu pamene Simei ankapita mbali inai m'mphepete mwa phiri, kutukwana kuli m'kati. Ndipo ankaponya miyala Davide ndi kumamuwazanso dothi. Tsono mfumu ndi anthu onse amene anali naye, adafika ku Yordani ali otopa kwambiri, napumula kumeneko. Abisalomu ndi Aisraele onse amene anali naye, kudzanso Ahitofele, adaaloŵa mu Yerusalemu. Ndipo pamene Husai Mwariki, bwenzi la Davide, adakumana ndi Abisalomu, adafuula kwa Abisalomuyo kuti, “Amfumu akhale ndi moyo wautali! Amfumu akhale ndi moyo wautali!” Tsono Abisalomu adafunsa Husai kuti, “Kodi ndimo m'mene umamkondera bwenzi lako? Chifukwa chiyani sudapite naye limodzi bwenzi lakoyo?” Apo Husai adayankha Abisalomu kuti, “Iyai, munthu amene wasankhidwa ndi Chauta ndiponso ndi anthu aŵa, kudzanso amuna onse a Aisraele, ndiye ndidzakhale mtumiki wake, ndipo ndidzakhala pambuyo pake. Nanganso ndani amene ine ndingamtumikire? Kodi si inuyo mwana wa mfumu? Monga momwe ndidatumikira bambo wanu, momwemonso ndidzakutumikirani inu.” Tsono Abisalomu adafunsa Ahitofele kuti, “Iwe ukuganiza bwanji pamenepa? Tsopano tichite chiyani?” Ahitofele adauza Abisalomu kuti, “Pitani mukaloŵe kwa azikazi a bambo wanu amene adaŵasiya kuti azisunga mudzi. Aisraele onse akadziŵa kuti bambo wanu akuipidwa nanu, onse amene akukutsataniŵa adzalimba mtima.” Motero adamangira Abisalomu hema pa denga la nyumba ya mfumu. Ndipo Abisalomu adapita kukaloŵa kwa azikazi a bambo wake, Aisraele onse akupenya. Tsono masiku amenewo, malangizo amene ankapereka Ahitofele anali ngati mau ochokera kwa Mulungu. Choncho uphungu wonse wa Ahitofele ankaulemekeza Davide ndi Abisalomu yemwe. Pambuyo pake Ahitofele adauza Abisalomu kuti, “Mundilole ndisankhule anthu okwanira 12,000, ndinyamuke nawo kuti ndimthamangire Davide usiku uno. Tsono ndikamthira nkhondo atatopa ndiponso atataya mtima, ndipo ndikamchititsa mantha. Anthu onse amene ali naye adzathaŵa. Pamenepo ine ndidzangopha mfumu yokhayo. Tsono anthu onse ndidzabwera nawo kwa inu, ngati mkwati amene akubwerera kwa mwamuna wake. Imfa ya munthu mmodzi yekha, idzakhalitsa anthu onse pa mtendere.” Uphunguwo udakomera Abisalomu ndi atsogoleri onse a Aisraele. Apo Abisalomu adati, “Muitanenso Husai, Mwariki, ndipo timvenso zimene anene.” Husai atabwera kwa Abisalomu, Abisalomuyo adamuuza kuti, “Zimene wanena Ahitofele nzimenezi, kodi tichitedi monga m'mene watilangiziramo? Ngati si choncho, iweyo utiwuze chochita.” Husai adauza Abisalomu kuti, “Ulendo uno, malangizo amene wakupatsani Ahitofele si abwino konse. Mukudziŵa kuti bambo wanu ngwamphamvu, anthu akenso ngamphamvu, ndipo kuti onse ngokwiya ngati zimbalangondo zolandidwa ana ku thengo. Kuwonjezera pamenepo, bambo wanu ndi katswiri wa nkhondo. Sangagone pamodzi ndi anthu ake ankhondo usiku. Onani, ngakhale tsopano lino akubisala m'phanga lina, kapena ku malo ena ake. Motero ena mwa anthu anu atangophedwa poyamba pomwe, aliyense amene adzamve adzanena kuti, ‘Anthu amene ankatsata Abisalomu aphedwa.’ Tsono ngakhale munthu wolimba mtima ngati mkango adzaguluka m'nkhongono. Paja Aisraele onse akudziŵa kuti bambo wanu ndi munthu wamphamvu, ndipo kuti anthu amene ali nawowo ngolimba mtima. “Ine malangizo anga ndi aŵa: Aisraele onse adzasonkhane kwa inu kuno, kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba, adzakhale ochuluka ngati mchenga wa m'mbali mwa nyanja. Ndipo inu nomwe mudzapite nawo ku nkhondo. Tsono ife tidzampeza Davide kulikonse kumene adzapezeke, ndipo tidzamthira nkhondo monga m'mene mame amagwera ponseponse pa nthaka. Sipadzapulumuka ndi munthu mmodzi yemwe. Akakaloŵa mumzinda mwina, Aisraele onse adzabwera ndi zingwe kumzindako. Mzinda umenewo tidzauguzira ku chigwa, ndipo sipadzapezeka ndi kamwala komwe kumeneko.” Atamva zimenezi Abisalomu ndi Aisraele onse adati, “Malangizo koma aŵa a Husai Mwarikiyu, osati a Ahitofele aja ai.” Zidatero chifukwa Chauta ndiye adaakonza kuti malangizo abwino a Ahitofele alephereke, zinthu zisamuyendere bwino Abisalomu. Kenaka Husai adauza Zadoki ndi Abiyatara, ansembe aja, kuti, “Zimene Ahitofele adaalangiza Abisalomu ndi atsogoleri a Aisraele ndi izi, izi. Koma ineyo ndaŵalangiza izi, izi. Ndiye inu tsono mutumize mau mwamsanga kwa Davide omuuza kuti asagone pa madooko a Yordani ku chipululu. Koma mwa njira iliyonse, aoloke ndithu, kuti iye pamodzi ndi anthu onse amene ali naye angagwidwe ndi kuphedwa.” Tsono mwachizoloŵezi Yonatani ndi Ahimaazi ankadikira ku Enirogele, pafupi ndi Yerusalemu. Mdzakazi ndiye ankapita kukaŵauza zinthu, ndipo iwowo ankapita kukauza mfumu Davide. Pakuti iwowo sankayenera kuwonekera poloŵa mu mzinda. Koma tsiku lina mnyamata wina adaŵaona, nakauza Abisalomu. Choncho Yonatani ndi Ahimaazi adathaŵa mofulumira, nakafika ku Bahurimu ku nyumba ya munthu wina, amene anali ndi chitsime pakhomo pake. Aŵiriwo adatsikira m'chitsimemo. Tsono mkazi wa munthu uja adatenga chivundikiro, nachiika pamwamba pa chitsimecho, nkuyanikapo tirigu, kotero kuti chitsimecho sichinkadziŵika. Ankhondo a Abisalomu atabwera kwa mkaziyo kunyumba kuja, adamufunsa kuti, “Kodi mwaonako Ahimaazi ndi Yonatani pano?” Mkazi uja adaŵayankha kuti, “Amenewo aoloka mtsinjewu.” Koma ataŵafunafuna, osaŵapeza, ankhondowo adabwerera ku Yerusalemu. Ankhondo aja atapita, anthuwo adatuluka m'chitsime muja, ndipo adakauza mfumu Davide kuti, “Nyamukani, muwoloke mtsinje mofulumira, popeza kuti Ahitofele walangiza anthu ake zokuthirani nkhondo.” Pompo Davide adanyamukadi pamodzi ndi anthu onse amene anali naye, naoloka mtsinje wa Yordani. Pamene kunkacha, nkuti anthu onse atatha kuwoloka Yordani. Ahitofele ataona kuti anthu sadatsate malangizo ake aja, adakwera bulu wake, napita kwao ku mzinda wake. Tsono adakonza zonse za m'nyumba mwake, nadzikhweza. Motero adafa, ndipo adaikidwa m'manda a bambo wake. Davide adafika ku Mahanaimu. Abisalomu adaoloka Yordani pamodzi ndi Aisraele onse aja. Abisalomu adaaika Amasa kuti akhale mtsogoleri wa ankhondo m'malo mwa Yowabu. Amasa anali mwana wa munthu wina dzina lake Yetere Mwismaele, amene adaakwatira Abigala, mwana wa Nahasi, mlongo wa Zeruya amake a Yowabu. Tsono Aisraele pamodzi ndi Abisalomu adamanga zithando zankhondo m'dziko la Giliyadi. Davide atafika ku Mahanaimu, Sobi mwana wa Nahasi Mwamoni wochokera ku Raba, ndi Makiri mwana wa Amiyele wa ku Lodebara, ndiponso Barizilai Mgiliyadi wa ku Rogelimu, adabwera ndi mabedi ambiri, mabeseni ambiri, ziŵiya zadothi, tirigu, barele, ufa, tirigu wokazinga, nyemba ndi mphodza. Adabweranso ndi uchi, chambiko, nkhosa ndi mafuta olimba a mkaka wang'ombe. Zonsezi adabwera nazo kuti Davide adye pamodzi ndi anthu amene anali naye. Iwowo ankati, “Anthuŵa ali ndi njala, atopa ndipo ali ndi ludzu kuchipululuko.” Pambuyo pake Davide adasonkhanitsa anthu amene anali naye kuti aŵagaŵe m'magulu, ndipo adaŵaikira atsogoleri, ena olamulira anthu zikwi, ena olamulira anthu mazana. Ndipo Davide adatumiza gulu lankhondo ataligaŵa patatu, chigawo chimodzi cholamulidwa ndi Yowabu, china cholamulidwa ndi Abisai, mwana wa Zeruya, mng'ono wake wa Yowabu, china cholamulidwa ndi Itai Mgiti. Tsono mfumu idauza anthuwo kuti, “Inenso ndipita nao.” Koma anthuwo adati, “Inuyo simupita nao, chifukwa ife tikathaŵa, adani sadzatisamala. Ngati theka la ife lifa, iwo sadzasamalako za ife. Koma inu mukuposa anthu 10,000 mwa ife. Nchifukwa chake nkwabwino kwambiri kuti inu muzingotitumizira chithandizo kuchokera kumzindako.” Mfumu idaŵauza kuti, “Chilichonse chimene chikukomereni, ndidzachita.” Choncho mfumuyo idakaimirira pambali pa chipata nthaŵi imene gulu lonse lankhondo linkatuluka mazanamazana, ndiponso zikwizikwi. Ndipo mfumu idalamula Yowabu, Abisai ndi Itai kuti, “Mumlezere mtima mwanayo Abisalomu chifukwa cha ine.” Anthu onse adamva pamene mfumu inkalamula atsogoleri a ankhondo kunena za Abisalomu. Tsono ankhondo adatuluka kunka ku thengo kukamenyana ndi Aisraele. Ndipo nkhondo idachitikira ku nkhalango ya Efuremu. Aisraele adagonjetsedwa kumeneko ndi ankhondo a Davide. Motero tsiku limenelo adaphedwa anthu ambiri okwanira 20,000 onse pamodzi. Nkhondo idafalikira m'dziko lonselo, ndipo zoopsa zam'nkhalango zidapha anthu ambiri kuposa anthu ophedwa ndi lupanga. Mwadzidzidzi Abisalomu adakumana ndi ankhondo a Davide. Abisalomuyo anali atakwera pa bulu wake, ndipo buluyo adaloŵa kunsi kwa nthambi zochindikira za mtengo wa thundu. Pamenepo Abisalomu adatsalira ali lendee, mutu wake utapanika pa nthambiyo, pamene bulu ankakwerayo adapitirira. Munthu wina ataona zimenezo, adauza Yowabu kuti, “Ndamuwona Abisalomu ali lendee mu mtengo wa thundu.” Yowabu adafunsa munthuyo kuti, “Nanga bwanji sudamphere pomwepo? Ndikadakondwa ndipo ndikadakupatsa ndalama zasiliva khumi ndiponso lamba.” Koma munthuyo adauza Yowabu kuti, “Ngakhale ndikadalandira m'manja mwangamu ndalama zasiliva zokwanira 1,000, sindikadasamula dzanja langa kuti ndiphe mwana wa mfumu. Paja mfumu idakulamulani inu ndi Abisai ndi Itai, ife tilikumva, kuti, ‘Mumtchinjirize mwanayo Abisalomu chifukwa cha ine.’ Bwenzi nditanyoza mau a mfumuwo, pomupha mwana wake, ndipo zikadadziŵika, poti palibe kanthu kobisika pamaso pa mfumu, ndipo inu nomwe simukadanditeteza.” Apo Yowabu adati, “Ukunditayitsa nthaŵi!” Ndipo adatenga mikondo itatu m'manja mwake, nakabaya Abisalomu m'chifuŵa asanafe, akali lendee mu mtengo wa thunduwo. Pomwepo ankhondo khumi onyamula zida zankhondo za Yowabu, adazinga Abisalomu, namkantha mpaka kumupha. Pambuyo pake Yowabu adaliza lipenga loletsa nkhondo, ndipo ankhondo ake adabwerako kumene ankalondola Aisraele kuja. Ndipo ankhondowo adatenga mtembo wa Abisalomu, nakautaya m'chidzenje chachikulu m'nkhalango, naunjika mulu wa miyala padzenjepo. Aisraele onse adathaŵa, aliyense kuthaŵira kwao. Abisalomu akadali moyo, adaadzimangira chipilala m'chigwa cha mfumu, poti ankati, “Ine ndilibe mwana wamwamuna woti adzakhale chikumbutso cha dzina langa.” Adaatchula chipilalacho dzina lake lomwe, ndipo mpaka pano chikutchulidwa kuti chikumbutso cha Abisalomu. Tsono Ahimaazi, mwana wa Zadoki, adati, “Imani ndithamange ndikauze mfumu nkhani yokondwetsayi yakuti Chauta waipulumutsa mfumuyo kwa adani ake.” Yowabu adauza Ahimaaziyo kuti, “Iwe usakanene zimenezi lero. Ukanene zimenezi tsiku lina, koma lero usakanene mbiri iliyonse, chifukwa mwana wa mfumu waphedwa.” Pambuyo pake Yowabu adauza Mkusi kuti, “Pita, ukauze mfumu zimene waziwonazi.” Mkusiyo adaŵeramira Yowabu mwaulemu, nayamba kuthamanga. Zitatero, Ahimaazi uja, mwana wa Zadoki, adauzanso Yowabu kuti, “Zitanizitani, mundilole kuti inenso ndimthamangire Mkusi uja.” Yowabu adamufunsa kuti, “Mwana wanga, chifukwa chiyani ukuti uthamange, pamene sudzalandirapo mphotho chifukwa cha uthenga umenewo?” Ahimaazi adati, “Zitanizitani, ine ndithamanga ndithu.” Apo Yowabu adamuuza kuti, “Chabwino, pita.” Choncho Ahimaazi adathamanga, kudzera njira yakuchigwa, nkumubzola Mkusi uja. Nthaŵi imeneyo nkuti Davide atakhala pakati pa zipata ziŵiri, chakubwalo ndi cham'kati. Mlonda adakwera pa khoma nakaimirira pa denga la chipata. Adati atayang'ana, adaona munthu akuthamanga yekhayekha. Ndipo mlondayo adafuula nauza mfumu. Mfumuyo idati, “Ngati ali yekhayekha, ndiye kuti ali ndi nkhani yabwino.” Tsono munthu uja adafika ndithu, nayandikira pafupi. Mlondayo adaona munthu winanso akuthamanga. Ndipo adafuulira munthu wapachipata nati, “Onani, pali munthu winanso akuthamanga yekhayekha.” Apo mfumu idati, “Iyeyonso akubwera ndi nkhani yabwino.” Mlonda uja adati, “Munthu akuthamanga patsogoloyo, kathamangidwe kake kakufanafana ndi m'mene amathamangira Ahimaazi, mwana wa Zadoki.” Mfumu idati, “Ameneyo ndi munthu wabwino, ndipo akubwera ndi nkhani yabwino.” Tsono Ahimaazi adafuula kwa mfumu, kuti, “Nkwabwino!” Atatero adadzigwetsa pansi pamaso pa mfumu, nati, “Atamandike Chauta, Mulungu wanu, amene wapereka m'manja mwanu anthu amene adaaukira inu mbuyanga mfumu.” Mfumu idamufunsa kuti, “Kodi mwana uja Abisalomu, zinthu zamuyendera bwino?” Ahimaazi adauza mfumu kuti, “Pamene Yowabu amandituma ine, kapolo wanu, ndinaona chipiringu chachikulu cha anthu, sindikudziŵa kaya kwagwa zotani.” Pompo mfumu idati, “Patuka, kaime apo.” Iye adapatuka nakaima potero. Mkusi uja nayenso adafika, ndipo adati, “Ndakutengerani uthenga wabwino, mbuyanga mfumu. Lero lino Chauta wakupulumutsani ku mphamvu za anthu onse amene ankakuukirani.” Tsono mfumuyo idafunsa Mkusi uja kuti, “Kodi mwana uja Abisalomu zinthu zamuyendera bwino?” Mkusiyo adayankha kuti, “Adani anu mbuyanga mfumu, pamodzi ndi anthu onse amene amakuukirani, ziŵaonekere zomwe zamuwonekera mwanayo.” Pamenepo mfumu idagwidwa ndi chisoni chachikulu, nikwera ku chipinda cham'mwamba pa chipata kukalira. Tsono popita inkati, “Iwe mwana wanga Abisalomu, mwana wanga Abisalomu. Kalanga ine, achikhala ndidaafa ndine m'malo mwako! Iwe Abisalomu mwana wanga, mwana wanga!” Anthu ena adauza Yowabu kuti, “Amfumutu akulira maliro a Abisalomu.” Choncho chikondwerero cha tsikulo chidasanduka maliro kwa anthu onse, pakuti anthu adamva kuti mfumu ili pa chisoni chachikulu chifukwa cha mwana wake. Tsiku limenelo anthu adaloŵa mu mzinda kachetechete, monga momwe anthu amaloŵera mu mzinda mwamanyazi, akamathaŵa kunkhondo. Mfumu idaphimba kumaso, nimalira kuti, “Kalanga ine, mwana wanga Abisalomu, iwe Abisalomu mwana wanga, mwana wanga!” Tsono Yowabu adaloŵa m'nyumba ya mfumu nakafika kwa mfumu, nati, “Inu lero mwachititsa manyazi ankhondo anu amene apulumutsa moyo wanu, ndiponso moyo wa ana anu aamuna ndi aakazi, kudzanso moyo wa akazi anu ndi wa azikazi anu, poti inu mumakonda anthu odana nanu, ndipo mumadana ndi anthu okukondani. Lero ndiye mwatiwonetsa poyera kuti akalonga ndi ankhondo anu mulibe nawo kanthu. Ha, ndikudziŵa kuti Abisalomu adakakhala moyo, tonsefe nkufa, inu mukadakondwa. Koma nyamukani tsono mutuluke, mukaŵalimbitse mtima ankhondo anu moŵakondweretsa. Ndithu ndikulumbira pali Chauta kuti, ngati simupita, onse akuthaŵani usiku uno. Ndipo zimenezi zidzakuipirani kwambiri kupambana zoipa zonse zimene zidakugweranipo kale, kuyambira muli mwana mpaka tsopano lino.” Itamva zimenezi mfumu idanyamuka, nikakhala pansi pafupi ndi chipata. Choncho anthu onse atamva kuti mfumu ili ku chipata, adabwera pamaso pa mfumuyo. Nthaŵi imeneyo nkuti Aisraele atathaŵa, aliyense kunka kwao. Ndipo onsewo ankangokangana okhaokha. Ankati, “Mfumu Davide adatipulumutsa kwa adani athu, ndipo adatilanditsa kwa Afilisti. Koma tsopano watuluka m'dziko muno, kuthaŵa Abisalomu. Koma Abisalomuyo amene ife tidamdzoza kuti akhale mfumu yathu, adafa ku nkhondo. Chifukwa chiyani tsono simukunena kanthu zokatenga mfumu Davide kuti abwerenso?” Mfumu Davide adatumiza mau kwa ansembe aja, Zadoki ndi Abiyatara, akuti, “Mufunse atsogoleri a ku Yuda kuti, ‘Chifukwa chiyani inu mukuzengereza kwambiri osakaitenganso mfumu kuti ibwerere ku nyumba kwake, pamene Aisraele onse atumiza kale mau kwa mfumu onena kuti mfumu ibwerere kunyumba kwake? Inu ndinu abale anga enieni. Chifukwa chiyani inuyo mukufuna kukhala otsirizira pakuiitananso mfumu?’ Ndipo mukauze Amasa mau anga oti, ‘Kodi iwe, sindiwe mbale wanga weniweni?’ Ndithu Mulungu andilange, mpaka ndife ndithu, ngati sindikuika iwe kuti ukhale mkulu wankhondo m'malo mwa Yowabu kuyambira tsopano lino.” Choncho Davide adakopa mitima ya Ayuda onse, ndipo adamangana chimodzi. Motero anthuwo adatumiza mau kwa mfumu kuti, “Bwererani inu pamodzi ndi ankhondo anu onse.” Motero mfumu idabwerera ku Yordani. Ndipo anthu onse a mtundu wa Yuda adafika ku Giligala kudzakumana ndi mfumu ndi kuiwolotsa Yordani. Tsono Simei, mwana wa Gera, Mbenjamini wa ku Bahurimu, adabwera mofulumira pamodzi ndi Ayuda kudzakumana ndi mfumu Davide. Iyeyo anali ndi anthu 1,000 a ku Benjamini. Zibanso mtumiki uja wa m'banja la Saulo, pamodzi ndi ana ake aamuna khumi ndi asanu ndiponso antchito ake makumi aŵiri, adathamangira ku Yordani, nakafikako isanafike mfumu. Ndipo adaolotsa onse a m'banja la mfumu, nachita zonse zokondweretsa mfumuyo. Tsono pamene mfumu Davide anali pafupi kuwoloka Yordani, Simei mwana wa Gera, adadzigwetsa pansi pamaso pa mfumuyo. Adauza mfumu kuti, “Mbuyanga, chonde mundikhululukire, musakumbukirenso tchimo limene ine kapolo wanu ndidachita pa tsiku lija, pamene inu mbuyanga mfumu munkachoka mu Yerusalemu. Amfumu musazisunge kukhosi zimenezi. Ine kapolo wanu ndikudziŵa kuti ndidalakwa. Nchifukwa chake mukuwona kuti ndabwera lero lino, ndipo m'banja lonse la Yosefe, ndayambira ndine kubwera kudzakuchingamirani inu mbuyanga mfumu.” Pompo Abisai, mwana wa Zeruya, adafunsa kuti, “Kodi Simeiyu ndiye saphedwa chifukwa chotukwana wodzozedwa wa Chauta?” Koma Davide adayankha kuti, “Za ine zikukukhudzani bwanji, inu ana a Zeruya, kuti lero lino mukhale ngati adani anga. Kodi lero m'dziko la Israele nkuphamo munthu? Kodi sindikudziŵa kuti tsopano ndine mfumu ya Aisraele?” Ndipo mfumu idauza Simei kuti, “Ndikunenetsa molumbira kuti iwe Simei suphedwa.” Tsono Mefiboseti, mdzukulu wa Saulo, adapita kukakumana ndi mfumu. Sadasambe m'miyendo, ndevu osameta, ndipo sadachape zovala zake kuyambira tsiku limene mfumu idachoka, mpaka tsiku limene idabwerera mwamtendere. Ndiye pamene ankabwera ku Yerusalemu kudzakumana ndi mfumu, mfumuyo idamufunsa kuti, “Iwe Mefiboseti, chifukwa chiyani sudapite nane limodzi?” Mefiboseti adayankha kuti, “Ine mbuyanga mfumu, adaandilakwitsa ndi wantchito wanga. Kapolo wanune wantchitoyo ndidamuuza bwinobwino kuti, ‘Undimangire chishalo pa bulu kuti ndikwere, ndipite nawo limodzi amfumu,’ poti paja ine kapolo wanu ndine wolumala. Koma iyeyo nkundisinjirira ine kapolo wanu kwa inu mbuyanga mfumu. Komatu inu muli ngati mngelo wa Mulungu. Nchifukwa chake tsono, muchite zimene zikukomereni. Paja anthu onse a banja la bambo wanga anali oyenera kuphedwa ndi inu mbuyanga mfumu. Koma ine mtumiki wanu mudaandiika pakati pa anthu amene ankadya ndi inu pa tebulo lanu. Nanga ndingakhale ndi chiyaninso ine chimene chingandiyenereze kuti ndingadandaule kwa inu amfumu?” Apo mfumu idati, “Basi ndamva usaonjezenso mau ena ai. Ine ndikufuna kuti iwe ndi Ziba mugaŵane chuma cha Saulo.” Koma Mefiboseti adauza mfumu kuti, “Mloleni mnzangayu kuti atenge ndiye chuma chonsecho. Kwa ine kwakwana kuti inu mbuyanga mfumu mwafika kwanu kuno mwamtendere.” Tsono Barizilai Mgiliyadi adafika kuchokera ku Rogelimu. Adapita ndi mfumu mpaka ku Yordani kuti akaiperekeze pooloka Yordani. Barizilai anali munthu wokalamba, wa zaka 80 zakubadwa. Ndipo iye ndiye ankapatsa mfumu chakudya nthaŵi imene mfumuyo inkakhala ku Mahanaimu, pakuti iyeyo anali munthu wolemera kwambiri. Choncho mfumu idauza Barizilai kuti, “Tiye tipite limodzi, ndikakusunga ku Yerusalemu.” Koma Barizilai adafunsa mfumu kuti, “Kodi ine zanditsalira zaka zingati zokhalabe moyo, kuti ndingapite nanu amfumu ku Yerusalemu? Tsopano ine zaka zanga zakwana 80. Kodi ndingathe kusiyanitsa zinthu zokondwetsa ndi zosakondwetsa? Kodi ine mtumiki wanu ndingathe kuzindikira kukoma kwake kwa zakudya kapena zakumwa? Kodi ine ndingathebe kumamvera kuimba kwa amuna ndi kwa akazi? Chifukwa chiyani ine mtumiki wanu ndikakhale ngati katundu wolemera wosanjikiza pa inu, mbuyanga mfumu? Koma ine mtumiki wanu ndingoyenda pang'ono kuti ndiwoloke Yordani pamodzi ndi inu amfumu. Amfumu mungandipatsirenji mphotho yotere? Chonde, ingondilolani ine mtumiki wanu ndibwerere kuti ndikafere kumudzi kwathu, pafupi ndi manda a bambo wanga ndi a mai wanga. Koma suyu mwana wanga Kimuhamu, akhale mtumiki wanu. Iyeyu ndiye aoloke pamodzi ndi inu mbuyanga mfumu. Ndipo mumchitire chilichonse chimene chikukomereni.” Apo mfumu idayankha kuti, “Kimuhamu ndiwoloka naye limodzi, ndipo ndidzamchitira chilichonse chimene chikukomereni inu. Ndipo zonse zimene mufuna kuti ndikuchitireni, ndidzakuchitirani.” Choncho anthu onse adaoloka Yordani, nayonso mfumu idaoloka. Ndipo mfumu idampsompsona Barizilai, nimdalitsa, ndipo iye adabwerera kwao. Mfumu idapitirira mpaka kukafika ku Giligala, ndipo Kimuhamu adapita nao. Anthu onse a ku Yuda ndiponso theka la anthu a ku Israele, onse adaperekeza mfumu. Kenaka Aisraele onse adafika kwa mfumu, nadzafunsa kuti, “Chifukwa chiyani abale athu Ayuda achita ngati kukubani, nabwera ndi inu amfumu pamodzi ndi banja lanu ndi anthu anu onse, kuwoloka Yordani?” Ayuda adayankha Aisraelewo kuti, “Chifukwa chake nchakuti mfumuyi ndi mbale wathu weniweni. Inu chakukwiyitsani nchiyani pamenepa? Kodi mfumu taidyera chiyani? Nanga yatipatsa mphatso yanji?” Apo Aisraelewo adayankha Ayuda aja kuti, “Tili ndi zigawo khumi mwa mfumu imeneyi, ndipo mwa ufumu wa Davide ife tili ndi zigawo zambiri kupambana inu. Nanga chifukwa chiyani tsono mukutinyoza? Kodi ife sindife amene tidayamba kulankhula zoti mfumu yathu ibwerenso?” Koma anthu a ku Yuda adalankhula mwaukali kwambiri kupambana anthu a ku Israele. Zidangochitika kuti kumeneko kunali munthu wina wachabechabe dzina lake Sheba, mwana wa Bikiri wa fuko la Benjamini. Iyeyo tsiku lina adaliza lipenga, nati, “Ife tilibe chathu mu ufumu wa Davide, tilibe choloŵa mwa mwana wa Yese! Inu Aisraele, aliyense apite kunyumba kwake!” Choncho Aisraele onse adaleka kumtsata Davide, nayamba kutsata Sheba, mwana wa Bikiri. Koma anthu a ku Yuda adakhalabe nganganga pambuyo pa mfumu yao, kuyambira ku Yordani mpaka ku Yerusalemu. Davide atafika ku nyumba yake ku Yerusalemu, adatenga azikazi ake khumi amene adaaŵasiya kuti azisunga mudzi, naŵatsekera m'nyumba m'mene adaaikamo mlonda woŵalonda. Ankaŵapatsa chakudya, koma Davide sankaloŵa m'nyumbamo kwa akaziwo. Adaŵatsekera m'nyumba choncho mpaka tsiku la kufa kwao, ndipo ankakhala ngati akazi amasiye. Tsono mfumu idauza Amasa kuti, “Itanire anthu onse a ku Yuda, abwere kuno pasanapite masiku atatu, ndipo iweyo udzakhalepo.” Motero Amasa adakaitana Ayuda. Koma adachedwa, napitiriza nthaŵi imene adaamuikira. Pamenepo Davide adauza Abisai kuti, “Sheba, mwana wa Bikiri, adzativuta kwambiri kupambana Abisalomu. Tenga ankhondo anga mulondole Shebayo kuti angadzipezere mizinda yamalinga namativutitsa.” Choncho Abisai uja, pamodzi ndi ankhondo a Yowabu, ndi Akereti, ndi Apeleti, ndi anyonga onse, adatuluka ku Yerusalemu kumalondola Sheba, mwana wa Bikiri. Nthaŵi imene adafika ku mwala waukulu umene uli ku Gibiyoni, Amasa adabwera kudzakumana nawo. Tsono Yowabu adaavala malaya ankhondo, ndipo pamwamba pa malayawo m'chiwuno mwake, panali lamba womangirirapo lupanga lam'chimake. Pamene ankayenda, lidasololoka. Tsono Yowabu adafunsa Amasa kuti, “Kodi nkwabwino mbale wanga?” Pamenepo Yowabuyo adamgwira ndevu Amasa uja ndi dzanja lake lamanja kuti amumpsompsone. Koma Amasa sadaachenjera nalo lupanga limene linali m'dzanja lina la Yowabu. Pomwepo Yowabuyo adamubaya nalo lupangalo m'mimba kamodzi kokha, mpaka matumbo ake kukhuthuka, naafa pomwepo. Tsono Yowabu ndi Abisai mbale wake adalondola Sheba mwana wa Bikiri. Wina mwa ankhondo a Yowabu adakaimirira pambali pa mtembo wa Amasa, nati, “Aliyense wokhumba Yowabu ndi Davide, mlekeni atsate Yowabuyo.” Monsemo nkuti Amasa atagona pa mseu ndi kuvimvinizika m'magazi ake. Ndipo aliyense amene ankabwera, ankati akamuona, nkuima. Tsono munthu wa Yowabu uja ataona kuti anthu akuima, adanyamula Amasa uja, kumchotsa mumseumo, nakamuika ku thengo, nkumfunditsa chovala. Amasayo atachotsedwa pamseupo, anthu onse adatsatira Yowabu, kuti alondole Sheba mwana wa Bikiri. Sheba adapita ndithu kubzola mafuko onse a Aisraele mpaka kukafika ku Abele wa ku Betemaki. Abikiri onse adasonkhana, naloŵa naye mumzindamo. Ndipo anthu onse amene anali ndi Yowabu adabwera, nadzamzinga ndi zithando zankhondo Shebayo ku Abele wa ku Betemaki. Tsono adauundira mitumbira yankhondo mzindawo, nikagunda ku linga. Choncho ankagumula khoma kuti aligwetse. Ndiye mkazi wina wanzeru adayamba kuitana mumzindamo kuti, “Tamverani! Tamverani! Tauzani aYowabu abwere kuno kuti ndilankhule nawo.” Yowabuyo adadza pafupi ndi mkaziyo, ndipo mkazi uja adamufunsa kuti, “Kodi inu ndinu aYowabu?” Yowabu adayankha kuti, “Ndine amene.” Mkaziyo adamuuza kuti, “Pepani bambo, mumvere mau anga.” Apo Yowabu adayankha kuti, “Inde, ndilikumva!” Apo mkazi uja adati, “Paja anthu kale ankati, ‘Kapempheni nzeru ku Abele.’ Nkhani zao ankazitha motero. Ife ndife anthu amtendere ndi okhulupirika m'dziko la Israele. Inu mukufuna kuwononga mzinda umene uli ngati mai m'dziko la Israele. Chifukwa chiyani mukuti mufafanize choloŵa cha Chauta?” Yowabu adayankha kuti, “Iyai, ine sindikufuna konse kuwononga mzinda uno. Cholinga si chimenechi. Koma munthu wina wa ku dziko la mapiri la Efuremu, dzina lake Sheba, mwana wa Bikiri, adaukira mfumu Davide. Mumpereke yekhayo, ndipo mzindawu ndiwuleka.” Mkazi uja adauza Yowabu kuti, “Tikuponyerani mutu wake pa khoma.” Kenaka mkaziyo mwa nzeru zake adapita kwa anthu, naŵasimbira nkhaniyi. Choncho anthuwo adadula mutu wa Sheba, mwana wa Bikiri, namponyera Yowabu. Pamenepo Yowabu adaliza lipenga, ndipo ankhondo ake adachoka kumzindako, aliyense kupita kwao, ndipo Yowabu adabwerera ku Yerusalemu kwa mfumu. Yowabu ankalamulira gulu lonse lankhondo la Aisraele. Ndipo Benaya, mwana wa Yehoyada, ankalamulira Akereti ndi Apeleti. Adoniramu anali mkulu woyang'anira za thangata. Yehosafati, mwana wa Ahiludi, anali mlembi wolemba mbiri ya dziko. Seva anali mlembi wa mfumu. Zadoki ndi Abiyatara anali ansembe. Ndipo Ira Myairi nayenso anali wansembe wa Davide. Nthaŵi ya ufumu wa Davide kunali njala ya zaka zitatu motsatanatsatana. Ndiye Davide adapempha nzeru kwa Chauta, ndipo Chauta adamuuza kuti, “Saulo ndi banja lake adakali nawobe mlandu uja wopha Agibiyoniwu.” Choncho mfumuyo idaitana Agibiyoni. Agibiyoniwo sanali Aisraele, koma Aamori otsalira. Ngakhale Aisraele anali atalumbira kuti sadzaŵapha Agibiyoniwo, komabe Saulo adafuna kuŵaonongeratu chifukwa cha chikondi chake pa Israele ndi pa Yuda. Tsono Davide adafunsa Agibiyoni aja kuti, “Kodi ndikuchitireni chiyani? Ndingapepese bwanji kuti mutipemphere kwa Chauta kuti atidalitse?” Agibiyoniwo adauza Davide kuti, “Mlandu umene ulipo pakati pa ife ndi Saulo kapena banja lake, si woti nkulipira ndi golide kapena siliva, ndiponso sikuti kapena ife tikufuna kulipira pakupha wina aliyense m'dziko la Israele ai.” Apo Davide adafunsanso kuti, “Nanga tsono mukuti ndikuchitireni chiyani?” Iwo adayankha kuti, “Saulo adaafuna kutiwonongeratu, ndipo adaakonza zoti titheretu m'dziko lonse la Israele. Tsono mwa zidzukulu zake mutipatse anthu asanu ndi aŵiri, kuti ife tikaŵanyonge pamaso pa Chauta ku Gibiyoni, ku mzinda wa Saulo munthu wosankhidwa wa Chauta.” Apo mfumuyo idayankha kuti, “Chabwino, ndidzaŵapereka.” Koma mfumu idasunga Mefiboseti, mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, chifukwa cha kulumbira kumene mfumu Davideyo ndi Yonatani mwana wa Saulo adaachita pamaso pa Chauta. Choncho mfumuyo idatenga Arimoni ndi Mefiboseti winanso, ana a Rizipa, mwana wamkazi wa Aya amene adambalira Saulo. Idatenganso ana aamuna asanu amene Merabi, mwana wamkazi wa Saulo, adambalira Adriyele mwana wa Barizilai Mmehola, naŵapereka kwa Agibiyoni. Tsono onsewo adaŵanyonga pa phiri, pamaso pa Chauta, ndipo asanu ndi aŵiri onsewo adafera pamodzi. Iwowo adaphedwa masiku oyamba akholola, nthaŵi yoyamba kudula barele. Tsono Rizipa, mwana wamkazi wa Aya, adatenga chiguduli nadziyalira pathanthwe pamene panali mitembo ya anthuwo, kuyambira pa chiyambi cha kholola mpaka mvula idayambanso kugwa. Mkaziyo sadalole kuti pa mitemboyo pafike mbalame masana kapena zilombo zakuthengo usiku. Davide atamva zimene Rizipa mwana wa Aya, mzikazi wa Saulo adachita, adapita kukatenga mafupa a Saulo ndi mafupa a Yonatani mwana wa Saulo. Adaŵachotsa m'manja mwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi, amene adaaba mafupawo ku bwalo la ku Beteseani, kumene Afilisti adaaŵanyonga, tsiku limene Afilistiwo adapha Saulo ku Gilibowa. Davide adatenga mafupa a Saulo ndi a Yonatani mwana wake naŵachotsa kumeneko. Kenaka adasonkhanitsanso mafupa a anthu aja amene adaŵanyongera paphiri paja. Ndipo adaika mafupa a Saulowo pamodzi ndi mafupa a Yonatani mwana wake, m'dziko la Benjamini ku Zela, m'manda a Kisi bambo wake wa Saulo, potsata zonse zimene mfumu idaalamula. Pambuyo pake Mulungu adamvera mapemphero opempherera dzikolo. Nthaŵi ina Afilisti adamenyananso nkhondo ndi Aisraele. Davide adapita ndi ankhondo ake, nakamenyana nawo nkhondo Afilistiwo, ndipo iyeyo adatopa kwambiri. Tsono Isibi-Benobi, mmodzi mwa zidzukulu za ziphona zija zotchedwa Arefaimu, amene mkondo wake unkalemera makilogramu atatu ndi theka, ndiponso amene anali ndi lupanga latsopano m'lamba, adaganiza zoti aphe Davide. Koma Abisai, mwana wa Zeruya, adabwera kudzathandiza Davide, nalimbana ndi Mfilistiyo mpaka kumupha. Tsono anthu a Davide adamlonjeza molumbira Davideyo kuti, “Tsopano inu simudzapita nafenso ku nkhondo, kuwopa kuti mungaphedwe. Inu ndinu amene Aisraele onse amagonerapo.” Pambuyo pake nkhondo idabukanso ndi Afilisti ku Gobu. Pamenepo Sibekai Muhusa, adapha Safu, amene analinso mmodzi mwa zidzukulu za Arefaimu. Kenaka nkhondo inanso idabuka ndi Afilisti omwewo ku Gobu. Tsono Elihanani, mwana wa Yaare-Oregimu wa ku Betelehemu, adapha Lahimi, mbale wa Goliyati wa ku Gati uja, amene thunthu la mkondo wake linali lalikulu ngati mtanda woombera nsalu. Kudabukanso nkhondo ina ku Gati, kumene kunali munthu wina wamtali, wa zala zakumanja uku zisanu ndi chimodzi uku zisanu ndi chimodzi, zakumwendonso uku zisanu ndi chimodzi uku zisanu ndi chimodzi, zonse pamodzi zala 24. Iyeyonso anali mmodzi mwa zidzukulu za Arefaimu. Pamene iye ankanyoza Aisraele, Yonatani mwana wa Simea, mbale wa Davide, adamupha. Anthu anaiwo anali zidzukulu za Arefaimu a ku Gati, ndipo adaphedwa ndi Davide ndi ankhondo ake. Tsiku limene Chauta adaapulumutsa Davide kwa adani ake onse ndiponso kwa Saulo, Davideyo adaimbira Chauta nyimbo iyi yakuti, “Chauta ndiye thanthwe langa, linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndiye Mulungu wanga ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga. Ndiye linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndinu amene mumandiwombola pa nkhondo. Ndimaitana Chauta, amene ayenera kumtamanda, ndipo amandipulumutsa kwa adani anga. “Zoŵaŵa za imfa zidandizinga, mitsinje ya ku malo a anthu akufa idandisefukira. Nthambo zakumanda zidandizeŵeza, misampha ya imfa idandikola. “Ndidaitana Chauta m'zovuta zanga, ndidafuulira Mulungu wanga kuti andithandize. Iye ali m'Nyumba mwake adamva liwu langa, kulira kwanga kofuna chithandizo kudamveka kwa iye. “Pamenepo dziko lapansi lidanjenjemera ndi kuchita chivomezi. Maziko akumwamba adagwedezeka ndi kulilima chifukwa Chauta adaakalipa. M'mphuno mwake munkafuka utsi, m'kamwa mwake munkatuluka moto woononga, makala amoto anali laŵilaŵi kuchokera m'kamwa momwemo. Adang'amba thambo natsika pansi, mdima wabii unali ku mapazi ake. Adakwera pa mkerubi nauluka, adayenda mwaliŵiro ndi mphepo. Mdima adausandutsa chofunda chake, mitambo yakuda yamvula adaisandutsa mwafuli wake. M'kuŵala kumene kunali pamaso pake munkafumira makala amoto alaŵilaŵi. Kumwamba Chauta adagunda ngati bingu, Wopambanazonse liwu lake lidamveka. Adaponya mivi yake, nabalalitsa adani ake. Adachititsa zing'aning'ani, naŵapirikitsa. Ngalande zozama zam'nyanja zidaonekera, maziko a dziko lapansi adakhala poyera, pamene Chauta adakhuluma mokalipa, pamene adatulutsa mpweya wamphamvu m'mphuno mwake. “Ali kumwamba Chauta adatambalitsa dzanja nandigwira, ndi kundivuula m'madzi ozama. Adandipulumutsa kwa adani anga amphamvu, kwa onse amene ankadana nane; pakuti iwo anali amphamvu kwambiri kupambana ine. Adaniwo adandithira nkhondo pamene ndinali m'mavuto, koma Chauta adandichirikiza. Adakandifikitsa ku malo amtendere, adandipulumutsa chifukwa adakondwera nane. “Chauta adandipatsa mphotho molingana ndi kulungama kwanga, adandifupa molingana ndi ungwiro wanga. Ine ndidatsata njira za Chauta sindidachite zoipa ndi kumsiya Mulungu wanga. Ndidamvera malangizo ake onse, ndipo malamulo ake sindidaŵataye. Ndinalibe mlandu pamaso pake, ndinkalewa zoipa m'moyo wanga. Nchifukwa chake Chauta wandipatsa mphotho molingana ndi kulungama kwanga, monga momwe akuwonera kuti ndilibe mlandu. “Kwa anthu okhulupirika, Inu Mulungu mumadziwonetsa okhulupirika, kwa anthu aungwiro mumadziwonetsa abwino kotheratu. Kwa anthu oyera mtima mumadziwonetsa okoma mtima, koma kwa anthu oipa mtima mumadziwonetsa ochenjera koposa. Paja anthu odzichepetsa Inu mumaŵapulumutsa, koma anthu odzikuza mumaŵatsitsa. Ndithu Inu Chauta, ndinu nyale yanga, Inu Mulungu, mumandiwunikira mu mdima. Ndi chithandizo chanu ndingathe kugonjetsa gulu la ankhondo. Ndi chithangato chanu, Inu Mulungu, ndingathe kupambana. Mulungu wathuyo zochita zake nzangwiro, mau a Chauta ndi oona. Iye ndiye chishango choteteza onse othaŵira kwa Iye. “Palibe Mulungu wina koma Chauta yekha. Palibe thanthwe lina lothaŵirapo koma Mulungu wathu yekha? Mulungu wathu ndiye linga langa lolimba, wandichotsera zoopsa m'njira zanga. Amalimbitsa mapazi anga ngati a mbaŵala, ndipo amandisunga bwino ku mapiri. Amaphunzitsa manja anga kamenyedwe ka nkhondo, kotero kuti ndingathe kupinda uta wachitsulo. Inu mwanditeteza ndi chishango chanu chachipulumutso. Mwandikweza ndi chithandizo chanu. Mwalimbitsa miyendo yanga kuti ndiyende bwino, choncho mapazi anga sadaterereke. Ndidalondola adani anga ndi kuŵapeza, sindidabwerere mpaka nditaŵagonjetsa. Ndidaŵakantha, ndidaŵagwetsa pansi, kotero kuti sadadzukenso, ndidaŵapondereza ndi mapazi anga. Paja ndinu mudandipatsa mphamvu zomenyera nkhondo, ndinu mudandigonjetsera anthu ondiwukira. Inu mudapirikitsa adani anga kuti andithaŵe, amene ankadana nane ndidaŵaononga. Adakuwa, koma panalibe ndi mmodzi yemwe woŵapulumutsa. Adalirira Chauta, koma sadaŵayankhe. Ndidaŵaperapera ngati fumbi, ndidaŵaphwanya ndi kuŵapondereza ngati matope amumseu. “Mudandipulumutsa kwa anthu anga ondiwukira. Mudandisunga kuti ndikhale wolamulira mitundu yonse. Choncho anthu osaŵadziŵa adayamba kunditumikira. Anthu a maiko ena adabwera kwa ine kudzapemba; atangomva mau anga oyamba adandimvera. Anthu a mitundu ina adataya mtima, adatuluka m'malinga mwao ali njenjenje. “Chauta ndiwamoyo. Litamandike thanthwe langa, alemekezeke Mulungu wanga, thanthwe londipulumutsa. Mulungu ndiye adandithandiza kuti ndilipsire, ndi kugonjetsa anthu a mitundu ina kuti akhale mu ulamuliro wanga. Ndinu amene mudandipulumutsa kwa adani anga. Mudandikweza pamwamba pa ondiwukira, mudandilanditsa kwa anthu ankhanza. “Chifukwa cha zimenezi ndidzakuyamikani Inu Chauta, pakati pa mitundu ya anthu, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu. Mulungu amathandiza mfumu yake kuti izipambana nthaŵi ndi nthaŵi. Amaonetsa chikondi chake chosasinthika kwa wodzozedwa wake, ndiye kuti kwa Davide ndi kwa zidzukulu zake mpaka muyaya.” Naŵa mau otsiriza a Davide: Nayi nyimbo ya Davide, mwana wa Yese, mau a munthu amene Mulungu adamkweza pamwamba, amene Mulungu wa Yakobe adamdzoza kuti akhale mfumu, munthu wokonda kuimba nyimbo zokoma za Israele: “Mzimu wa Chauta ukulankhula mwa ine, mau ake ali pakamwa panga. Mulungu wa Israele walankhula, Thanthwe la Israele landiwuza kuti, ‘Munthu amene amalamulira anthu mwachilungamo, kuŵalamulira molemekeza Mulungu, amaŵafikira ngati kuŵala kwam'maŵa amaŵaŵalira ngati dzuŵa lam'maŵa pa tsiku lamitambo. Alinso ngati mvula imene imameretsa udzu pa nthaka.’ Motero Mulungu adzadalitsa zidzukulu zanga chifukwa Iye adachita nane chipangano chosatha, chipangano cholongosoka bwino ndi chosasinthika. Izi nzimene ndikulakalaka, ndiponso zimene zidzandipulumutsa. Ndi Mulungu amene adzachita zonsezi. Koma anthu oipa onse amachotsedwa ngati minga. Anthu satha kuigwira ndi manja. Koma amaidula ndi chigwandali nakaitentha pa moto.” Naŵa maina a ankhondo amphamvu a Davide: Yosebu-Basebeti, wa ku Takemoni, mkulu wa atsogoleri ankhondo atatu. Iye adaamenyana nkhondo ndi anthu 800, naŵapha onsewo ndi mkondo wake. Mnzake wotsatana naye mwa anthu atatu amphamvu aja anali Eleazara, mwana wa Dodo, mwana wa Aho. Iyeyo anali pamodzi ndi Davide pamene ankaputa Afilisti omwe adaasonkhana kuti amenyane naye nkhondo ku Pasi-Damimu. Aisraele anali atathaŵa. Koma iyeyo adatsalira, nakantha Afilisti mpaka dzanja lake kuchita kutopa, komabe osataya lupanga. Tsiku limenelo Chauta adampambanitsa. Aisraelewo adabwerera pambuyo pake kudzangofunkha za ophedwawo. Wotsatana ndi ameneyo anali Sama, mwana wa Age Muharari. Nthaŵi ina Afilisti adasonkhana ku Lehi kumene kunali munda wa mphodza. Aisraele nkuthaŵa Afilisti aja. Koma iyeyo adaima pakatimpakati pa mundawo nautchinjiriza, ndipo adapha Afilistiwo, chifukwa Chauta adampambanitsa kwambiri. Nthaŵi yokolola, atatu mwa ankhondo otchuka makumi atatu aja, adapita kwa Davide ku phanga la Adulamu, pamene gulu lankhondo la Afilisti linkamanga zithando zankhondo ku chigwa cha Refaimu. Pamenepo nkuti Davide ali m'phanga muja, ndipo kagulu kankhondo ka Afilisti kali ku Betelehemu. Tsono Davide adalankhula molakalaka kuti, “Ha, wina akadandipatsa madzi akumwa a m'chitsime chimene chili ku chipata ku Betelehemu kuti ndimwe!” Pamenepo anthu atatu amphamvu aja adapita, nabzola zithando za Afilisti, nkutunga madzi m'chitsime cha ku Betelehemu, chimene chinali pafupi ndi chipata. Adatenga madziwo, nabwera nawo kwa Davide. Koma Davideyo sadafune kumwako madziwo adangoŵathira pansi, kuŵapereka kwa Chauta, nati, “Ndithudi pali Chauta, sindingachite chinthu chotere, chifukwa kukhala ngati kumwa magazi a anthuŵa amene adaika moyo wao paminga.” Motero adakana kumwa madziwo. Zimenezi ndizo adachita anthu atatu amphamvu aja. Tsono Abisai, mbale wa Yowabu, mwana wa Zeruya, ndiye anali mtsogoleri wa anthu makumi atatu aja. Ndiye adapha anthu 300 ndi mkondo wake, nakhala wotchuka ngati anthu atatu ena aja. Iyeyo anali womveka kwambiri mwa atsogoleri makumi atatu aja, ndipo adasanduka mkulu wao. Komabe sadafikepo pa anthu atatu aja. Benaya mwana wa Yehoyada, wa ku Kabizeele, anali munthu wolimba mtima amene ankachita ntchito zamphamvu. Iyeyo adapha ankhondo aŵiri otchuka a ku Mowabu. Tsiku lina chisanu cha mbee chitagwa, adatsikira m'chitsime, naphamo mkango. Adaphanso Mwejipito wina, wa maonekedwe okongola. Mwejipitoyo adaali ndi mkondo m'manja, koma Benaya adapita kwa iyeyo ndi ndodo chabe. Adalanda mkondowo ku manja mwa Mwejipito uja, namupha ndi mkondo wake womwewo. Zimenezi ndi ntchito zimene adatchuka nazo Benaya mwana wa Yehoyada, yemwe anali m'modzi wa anthu makumi atatu amphamvu aja. Iyeyo anali womveka pakati pa atsogoleri makumi atatu aja, komabe sadafikepo pa anthu atatu aja. Davide adamuika kuti azilamulira asilikali ake omuteteza. M'gulu la anthu makumi atatu aja munalinso aŵa: Asahele, mbale wa Yowabu, Elihanani, mwana wa Dodo, wa ku Betelehemu, Sama wa ku Harodi, Elika wa ku Harodi Helezi Mpeleti, Ira mwana wa Ikesi wa ku Tekowa, Abiyezere wa ku Anatoti, Mebunai Muhusa, Zalimoni Mwahohi, Maharai wa ku Netofa, Helebi mwana wa Baana wa ku Netofa, Itai mwana wa Ribai wa ku Gibea, Mbenjamini. Panalinso Benaya wa ku Piratoni, Hidai wa ku mitsinje ya ku Gaasi, Abiyaliboni Mwaraba, Azimaveti wa ku Bahurimu, Eliyaba wa ku Saaliboni, ana a Yaseni, Yonatani, Sama Muharari, Ahiyamu mwana wa Sarara Muharari, Elipeleti mwana wa Ahasibai wa ku Maaka, Eliyamu mwana wa Ahitofele wa ku Gilo, Heziro wa ku Karimele, Paarai Mwaraba, Igala mwana wa Natani wa ku Zoba, Bani Mgadi, Zeleki Mwamoni, Naharai wa ku Beeroti, wonyamula zida za Yowabu, mwana wa Zeruya, Ira Mwitiri ndi Garebu Mwitiri ndi Uriya Muhiti uja. Onse pamodzi anali anthu 37. Nthaŵi ina Chauta adaŵakwiyiranso Aisraele, choncho adautsa mtima wa Davide kuti aŵavutitse. Adamuuza kuti, “Pita ukaŵerenge Aisraele ndi Ayuda.” Choncho mfumu Davide adauza Yowabu ndi atsogoleri ankhondo amene anali naye pamodzi kuti, “Pitani pakati pa mafuko onse a Aisraele kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba, mukaŵerenge anthu kuti ndidziŵe chiŵerengero chao.” Koma Yowabu adauza mfumu kuti, “Chauta Mulungu wanu achulukitse anthu makumi khumi kupambana m'mene alirimu, ndipo alole kuti inu mbuyanga mfumu mudzaziwone zimenezo. Koma chifukwa chiyani inu mbuyanga mfumu mukufuna chinthu chotere?” Komabe mau a mfumu adapambana mau a Yowabu ndi a atsogoleri ankhondo aja. Choncho Yowabu ndi atsogoleri ankhondowo adachokapo kuti akaŵerenge Aisraele. Adaoloka mtsinje wa Yordani, nayambira ku Aroere, mzinda umene uli pakati pa chigwa cha ku Gadi, mpaka ku Yazere. Tsono adafika ku Giliyadi ndi ku Kadesi m'dziko la Ahiti, nakafika ku Dani, kuchokera kumeneko adayenda mozungulira ku Sidoni. Ndipo adakafika ku linga la Tiro ndi ku mizinda yonse ya Ahivi, ndi ya Akanani. Atatero, adachoka kumeneko nakafika kumwera kwa Yuda, ku Beereseba. Motero, atabzola dziko lonselo, adadzafika ku Yerusalemu itatha miyezi isanu ndi inai ndi masiku makumi aŵiri. Tsono Yowabu adapereka chiŵerengero cha anthu onse kwa mfumu. Ku dziko la Israele kunali anthu 800,000 otha kumenya nkhondo, ndipo ku Yuda kunali 500,000 pamodzi. Pambuyo pake Davide adadzitsutsa mumtima mwake, atatha kaundulayo. Ndipo adapemphera kwa Chauta kuti, “Ndachimwa kwambiri pochita zimenezi. Koma tsopano, Inu Chauta, ndikukupemphani kuti mundikhululukire tchimo langa ine mtumiki wanu, popeza kuti ndachita zopusa kwambiri.” Tsono Davide atadzuka m'maŵa, Chauta adalankhula ndi Gadi, mneneri wa Davide, namuuza kuti, “Pita ukamuuze Davide kuti, ‘Ine Chauta ndikunena kuti, “Ndikuika pamaso pako zinthu zitatu zoti ndikuchite. Tsono usankhepo chimodzi, ndipo ndidzakuchita.” ’ ” Choncho Gadi adadza kwa Davide, namuuza kuti, “Musankhe, kodi pabwere zaka zitatu zanjala m'dziko mwanu, kapena inu mukhale mukuthaŵa adani anu pa miyezi itatu, kapena pakhale mliri wa masiku atatu m'dziko mwanu? Ganizani bwino, ndipo mutsimikize chilichonse choti muyankhe, kuti ine ndikauze amene adanditumayo.” Apo Davide adauza Gadi kuti, “Iyai, ine pamenepa ndavutika kwambiri mu mtima. Makamaka tigwe m'manja mwa Chauta, popeza kuti chifundo chake nchachikulu. Koma chonde, tisagwe m'manja mwa anthu ai.” Choncho Chauta adagwetsa mliri pa Aisraele, kuyambira m'maŵa mpaka pa nthaŵi imene adaafuna mwini wake, mwakuti kuchokera ku Dani mpaka ku Beereseba adafa anthu okwanira 70,000 pamodzi. Ndipo pamene mngelo adatambalitsa dzanja lake kuloza mzinda wa Yerusalemu kuti auwononge, Chauta adasintha maganizo achilangowo, nauza mngelo wake amene ankaononga anthu uja kuti, “Iyai, basi tsopano! Kwakwanira. Bweza dzanja lakolo.” Nthaŵi imeneyo nkuti mngelo wa Chautayo ataima pa malo opunthira tirigu a Arauna Myebusi. Davide adaona mngelo uja, ndipo adalankhula ndi Chauta, nati, “Ndachimwa ndine, ndipo ndachita choipa. Koma nkhosa izi kodi zachita chiyani? Amangonditsatira chabe. Tsono dzanja lanu likanthe ine ndi banja la bambo wanga.” Tsiku limenelo Gadi adafika kwa Davide namuuza kuti, “Mupite mukamangire Chauta guwa pa malo opunthira tirigu a Arauna Myebusi uja.” Atamva mau a Gadiwo, Davide adapita monga momwe Chauta adaalamulira. Ndipo Arauna atapenya chakunsi, adaona mfumu ikudza kwa iye pamodzi ndi atumiki ake. Pomwepo Araunayo adapita kukalambira mfumu choŵerama pansi. Tsono adafunsa mfumu kuti, “Bwanji mbuyanga mfumu, mukudza kwa ine mtumiki wanu?” Davide adati, “Ndikufuna kuti ndigule malo opunthira tirigu aja, kuti ndimangirepo Chauta guwa, kuti mliriwu uŵachoke anthu.” Arauna adauza Davide kuti, “Mbuyanga mfumu, mutenge mukapereke nsembe zinthu zimene zikukomereni. Nazi ng'ombe zokaperekera nsembe yopsereza. Nazinso zipangizo zomangira ng'ombe pamodzi ndi magoli omwe a ng'ombezo, kuti zikhale nkhuni.” Zonsezi Arauna adazipereka kwa mfumu, ndipo adapitiriza nati, “Chauta Mulungu wanu, alandire nsembe zanuzo.” Koma mfumu idauza Arauna kuti, “Iyai, koma ndichita chogula ndithu kwa iwe pa mtengo wake. Sindingapereke ngati nsembe zopsereza kwa Chauta Mulungu wanga zinthu zosagula.” Choncho Davide adagula malo opunthirapo tirigu aja pamodzi ndi ng'ombe zomwe pa mtengo wa masekeli asiliva makumi asanu. Ndipo kumeneko adamangako guwa, kumangira Chauta, napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Choncho Chauta adamva kupemba kwake kopembera dziko, ndipo mliriwo udaleka m'dziko la Israele. Mfumu Davide anali wokalamba kwambiri. Ndipo ngakhale ankamufunditsa mabulangete, sankamvabe kufunda. Nchifukwa chake nduna zake zidamuuza kuti, “Inu amfumu, tikupezereni namwali woti azikusungani ndi kumakusamalani. Namwaliyo azigona pafupi nanu kuti inu amfumu muzifundidwa.” Choncho adafunafuna namwali wokongola m'dziko lonse la Israele, ndipo adapeza Abisagi wa ku Sunamu, nabwera naye kwa mfumu. Namwaliyo anali wokongola kwambiri. Tsono adakhala wosamala mfumu ndi kumaitumikira. Koma mfumuyo sidakhale naye malo amodzi namwaliyo. Tsono Adoniya, mwana wa Hagiti, adayamba kudzikuza namanena kuti, “Ndidzakhala mfumu ndine.” Motero adadzipezera magaleta ndi anthu okwera pa akavalo, ndiponso anthu operekeza makumi asanu oti azithamanga patsogolo pake. Bambo wake Davide anali asanamdzudzulepo nkamodzi komwe pomufunsa kuti, “Kodi zakutizakutizi ukuchitiranji?” Adoniyayo anali wokongola, ndipo adaapondana ndi Abisalomu. Iyeyo adapangana ndi Yowabu, mwana wa Zeruya, ndiponso Abiyatara wansembe. Choncho iwowo adamtsata Adoniya namamthandiza. Koma Zadoki wansembe, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndiponso mneneri Natani, Simei, Rei, pamodzi ndi anthu amphamvu aja a Davide, sadamtsate Adoniyayo. Tsiku lina Adoniya adapereka nsembe za nkhosa, ng'ombe ndiponso anaang'ombe onenepa ku Mwala wa Njoka umene uli pafupi ndi Enirogele. Adaitana abale ake onse, ana a mfumu, ndi akazembe onse a ku Yuda. Koma sadaitaneko mneneri Natani, Benaya, anthu amphamvu aja a mfumu Davide, kapenanso Solomoni mbale wake. Natani adafunsa Bateseba, mai wa Solomoni, kuti, “Kodi simudamve kuti Adoniya, mwana wa Hagiti, wadzilonga ufumu, chikhalirecho Davide mbuyathu sakuzidziŵa zimenezo? Nchifukwa chake tsono ndikupatseni nzeru kuti mupulumutse moyo wanu pamodzi ndi moyo wa mwana wanu Solomoni. Pitani msanga kwa mfumu Davide, mukamfunse kuti, ‘Kodi inu mbuyanga mfumu, suja mudandilonjeza molumbira ine mdzakazi wanu, kuti mwana wanga Solomoni ndiye amene adzaloŵe ufumu m'malo mwanu nadzakhala pa mpando wanu m'malo mwanu? Nanga chifukwa chiyani Adoniya waloŵa ufumu?’ Tsono pamene inu muzikalankhula ndi mfumu, inenso ndidzaloŵa pambuyo panu, kuti ndikachitire umboni mau anuwo.” Choncho Bateseba adapita kwa mfumu, nakaloŵa m'chipinda chake. (Apo nkuti mfumuyo itakalamba kotheratu, ndipo Abisagi Msunamu uja ankasamala mfumuyo). Bateseba adagwada nalambira mfumu. Tsono mfumu idamufunsa kuti, “Kodi nkwabwino?” Bateseba adati, “Ai nkwabwino. Koma mbuyanga, paja inu mudaandilonjeza molumbira ine mdzakazi wanu m'dzina la Chauta Mulungu wanu kuti, ‘Solomoni mwana wako ndiye amene adzaloŵe ufumu m'malo mwanga, nadzakhala pa mpando wanga.’ Komabe tsono, onani, Adoniya wadzilonga ufumu, inuyo mbuyanga osazidziŵa zimenezo. Iyeyo wapha ng'ombe, anaang'ombe onenepa, ndiponso nkhosa zambiri, kuperekera nsembe, ndipo waitana ana anu onse, wansembe Abiyatara ndiponso Yowabu mkulu wankhondo. Solomoni mwana wanu sadamuitaneko ai. Mwakuti tsopano, mbuyanga mfumu, maso a Aisraele onse ali pa inu, kuti muŵauze munthu amene adzakhale pa mpando wanu waufumu, m'malo mwanu. Mukapanda kutero, zidzachitike nzakuti inu mbuyanga mutatisiya, kulondola kumene kudapita makolo anu, ine pamodzi ndi mwana wanga Solomoni adzatiyesa ogalukira mfumu.” Tsono Batesebayo akulankhula ndi mfumu, mneneri Natani adaloŵa. Anthu adauza mfumu kuti, “Kwafika mneneri Natani.” Tsono iye atafika pamaso pa mfumu, adaŵeramitsa mutu wake pansi. Ndipo adafunsa mfumu kuti, “Mbuyanga mfumu, kodi inu mudalengeza zoti Adoniya ndiye adzakhale mfumu ndi kukhala pampando panu? Pakuti lero lomwe lino wakapha ng'ombe, anaang'ombe onenepa, ndi nkhosa zambiri, kuperekera nsembe. Ndipo waitana ana anu onse pamodzi ndi Yowabu mkulu wa ankhondo, ndi wansembe Abiyatara. Onsewo akudya ndi kumwa naye Adoniyayo tsopano lino, ndipo akunena kuti, ‘Adzachite kufa ndi ukalamba mfumu Adoniya.’ Koma ine mtumiki wanu, wansembe Zadoki ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndiponso Solomoni mwana wanu, tonsefe sadatiitaneko. Kodi zimenezi mwalamula ndinu mbuyanga mfumu? Bwanji nanga simudauze anthu anu za mwana amene adzakhale pa mpando wanu waufumu m'malo mwanu?” Apo mfumu Davide adati, “Mundiitanire Bateseba, abwere kuno.” Bateseba adaloŵa, nakaimirira pamaso pa mfumu. Ndipo mfumu idalumbira kuti, “Pali Chauta wamoyo, amene adapulumutsa moyo wanga ku mavuto onse, monga momwe ndidaakulonjezera molumbira m'dzina la Chauta, Mulungu wa Israele, kuti mwana wako Solomoni ndiye amene adzaloŵe ufumu ndi kukhala pa mpando wanga, m'malo mwanga, ndikubwerezanso zomwezo lero.” Pomwepo Bateseba adaŵeramitsa mutu wake pansi nalambira mfumu, nati, “Mbuyanga mfumu Davide akhale ndi moyo mpaka muyaya!” Pamenepo mfumu Davide adati, “Mundiitanire wansembe Zadoki, mneneri Natani, ndi Benaya mwana wa Yehoyada.” Onsewo adafika pamaso pa mfumu. Tsono mfumu idaŵauza kuti, “Tengani anthu anga, ndipo mukweze Solomoni mwana wanga pa bulu wanga, mupite naye ku Gihoni. Kumeneko wansembe Zadoki ndi mneneri Natani akamdzoze kuti akhale mfumu yolamulira Israele. Kenaka mukalize lipenga, ndi kufuula kuti, ‘Achite kufa ndi ukalamba mfumu Solomoni.’ Tsono inu muzikamtsata pambuyo pobwerera kuno, kudzakhala pa mpando wanga waufumu. Iyeyo ndiye akhale mfumu m'malo mwanga. Ndamsankha iyeyo kuti akhale wolamulira Israele ndi Yuda.” Apo Benaya mwana wa Yehoyada adayankha kuti, “Indedi, zichitikedi motero. Chauta, Mulungu wa mbuyanga mfumu, akwaniritse zimenezi. Monga momwe Chauta wakhalira nanu mbuyanga mfumu, momwemonso akhale ndi Solomoni, ndipo ufumu wake aukweze ndithu, ngakhale kupambana ufumu wanu, mbuyanga mfumu Davide.” Tsono wansembe Zadoki, mneneri Natani ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndiponso Akereti ndi Apeleti oteteza mfumu aja, adapita nakamkweza Solomoni pa bulu wa mfumu Davide, kupita naye ku Gihoni. Kumeneko wansembe Zadoki adatenga nsupa ya mafuta ya ku hema la Chauta, nadzoza Solomoni. Pomwepo adaliza lipenga, ndipo anthu onsewo adafuula kuti, “Achite kufa ndi ukalamba mfumu Solomoni!” Anthuwo adapita namamtsatira pambuyo akuliza zitoliro ndi kukondwerera kwambiri, kotero kuti dziko lidagwedezeka chifukwa cha phokosolo. Pamene Adoniya ndi anthu onse oitanidwa amene anali naye ankamaliza madyerero ao, adalimva phokosolo. Yowabu atamva kulira kwalipenga, adafunsa kuti, “Kodi phokoso limeneli mumzindamo, kwachitikanji?” Akulankhulabe, adangoona Yonatani mwana wa wansembe Abiyatara wafika. Adoniya adamuuza kuti, “Loŵa, chifukwa ndiwe munthu wabwino, mwina mwake wabwera ndi uthenga wabwino.” Tsono Yonatani adayankha kuti, “Iyai, zinthu zaipa uku! Mbuyathu mfumu Davide walonga Solomoni ufumu. Adatuma wansembe Zadoki, mneneri Natani, ndi Benaya mwana wa Yehoyada ndiponso Akereti ndi Apeleti ku Gihoni. Ndipo iwo adamkweza Solomoniyo pa bulu wa mfumu. Tsono Zadoki wansembe uja ndi mneneri Natani adamdzoza Solomoni ku Gihoniko kuti akhale mfumu. Ndipo kuchokera kumeneko akhala akukondwerera, kotero kuti mumzinda monse muli phokoso. Ndiye lumbwe mwamvali. Solomoni wakhala pa mpando waufumu. Kuwonjezera pamenepo, nduna za mfumu zidadzamuyamika mbuyathu mfumu Davide nkumanena kuti, ‘Mulungu wanu akweze dzina la Solomoni kupambana dzina lanu, ndipo akweze ufumu wake kupambana ufumu wanu.’ Ndipo mfumu idaŵerama niyamba kupemphera pa bedi. Idati, ‘Atamandike Chauta, Mulungu wa Aisraele, amene lero walola kuti mmodzi mwa ana anga akhale pa mpando wanga waufumu, ine ndemwe ndikuwona.’ ” Pomwepo anthu onse amene Adoniya adaaŵaitana aja adayamba kunjenjemera, ndipo adamwazikana aliyense kumapita kwao. Pamenepo Adoniya adayamba kuwopa Solomoni. Adapita ku Nyumba ya Mulungu nakagwira nsonga za guwa lansembe. Tsono ena adauza Solomoni kuti, “Adoniya akukuwopani, inu mfumu Solomoni, ndipo wakagwira nsonga za guwa lansembe, ndipo akunena kuti poyamba afuna kuti inu mfumu Solomoni mulumbire kuti simudzamupha mtumiki wanuyo.” Solomoni adati, “Iyeyo akakhala womvera, sitimchita choipa chilichonse, koma akakhala woipa mtima, adzafa basi.” Kenaka mfumu Solomoni adatuma anthu kukamtenga Adoniya kuguwa kuja. Iye adabwera kudzalambira mfumu Solomoni. Ndipo Solomoni adamuuza kuti, “Chabwino, ungathe kupita kunyumba kwako.” Nthaŵi yoti Davide amwalire itayandikira, adauza mwana wake Solomoni kuti, “Ine ndi ulendo uno, nchifukwa chake tsono khala wamphamvu ndipo ulimbike mtima. Uzichita zimene Chauta Mulungu wako akulamula. Uziyenda m'njira za Chauta, uzimvera mau, malangizo ndi malamulo a Mulungu, monga momwe adalembedwera m'malamulo a Mose, kuti zonse zizikuyendera bwino kulikonse kumene ungapite. Uzitero kuti Chauta achitedi zimene adalankhula za ine kuti, ‘Ana ako aamuna akamasamala makhalidwe ao ndi kukhala okhulupirika kwa Ine ndi mtima wao wonse ndi mzimu wao wonse, sipadzasoŵa munthu pa banja lako wolamulira Israele.’ “Kuwonjezera pamenepo, ukudziŵanso zoipa zimene Yowabu mwana wa Zeruya adandichita, pakupha atsogoleri aŵiri a ankhondo a Aisraele aja, Abinere mwana wa Nere, ndi Amasa mwana wa Yetere. Kuteroko kunali kulipsira pa nthaŵi yamtendere magazi amene anthuwo adaakhetsa pa nthaŵi yankhondo. Koma tsopano ine pokhala mfumu, ndikusenza kuchimwa kwake ndi kuvala mlandu chifukwa cha magazi osachimwawo. Tsono iwe uchite potsata nzeru zako, koma ndithu usalole kuti afe ndi ukalamba ndi kupita ku manda mwamtendere. “Koma ana a Barizilai wa ku Giliyadi, uŵachitire zabwino ndi kuŵalola kuti azidya pamodzi nawe, poti adandichitira chifundo pamene adakumana nane nthaŵi imene ndinkathaŵa Abisalomu mbale wako. “Palinso Simei, mwana wa Gera, Mbenjamini wa ku Bahurimu, amene adaanditukwana momvetsa chisoni, tsiku limene ndinkapita ku Mahanaimu. Koma pamene adadza kudzakumana nane ku Yordani, ndidalumbira m'dzina la Chauta kuti sindidzamupha. Nchifukwa chake tsono usamuyese wosalakwa, poti iwe ndiwe munthu wanzeru. Udzadziŵa wekha choyenera kumchita. Ngakhale ndi nkhalamba, aphedwe ndithu.” Tsono Davide adamwalira, naikidwa m'manda mu mzinda wake wa Davideyo. Apo nkuti atalamulira Israele zaka makumi anai. Ku Hebroni adalamulira zaka zisanu ndi ziŵiri, ndipo ku Yerusalemu zaka 33. Choncho Solomoni adakhala pa mpando waufumu wa Davide atate ake. Ndipo ufumu wake unali wokhazikika kwambiri. Tsiku lina Adoniya, mwana wa Hagiti, adafika kwa Bateseba, mai wake wa Solomoni. Bateseba adamufunsa kuti, “Kodi wadzera mtendere?” Iye adati, “Ai, ndi zamtendere ndithu.” Tsono adati, “Koma ndili ndi mau oti ndilankhule nanu.” Bateseba adati, “Lankhula.” Adoniya adati, “Mukudziŵa kuti ufumuwu udaali wanga, ndipo Aisraele onse ankayembekeza kuti ndidzalamulira ndine. Koma zinthu zatembenuka, ufumuwo wapita kwa mbale wanga, popeza kuti adampatsa ndi Chauta. Tsopano ndikukupemphani chinthu chimodzi. Musandikanize ai.” Bateseba adati, “Nena.” Iyeyo adati, “Inuyo mfumu Solomoni sakukanizani, ndiye chonde ndimati mumpemphe kuti andipatse Abisagi, mtsikana wa ku Sunamu uja, kuti akhale mkazi wanga.” Bateseba adati, “Chabwino. Ndikulankhulira kwa mfumu.” Choncho Bateseba adapita kwa mfumu Solomoni kukalankhula naye m'malo mwa Adoniya. Solomoni adanyamuka kuti akumane naye, ndipo adaŵeramira mai wakeyo. Adakhala pa mpando wake waufumu, ndipo adaitanitsa mpando wina kuti mai wake akhalepo. Tsono mai uja adakhala ku dzanja lamanja la mfumuyo. Ndipo maiyo adati, “Ndikufuna kukupemphani kanthu kakang'ono. Chonde musandikanize.” Tsono mfumu idauza mai wakeyo kuti, “Pemphani chimene mukufuna, mai wanga, sindikukanizani.” Maiyo adati, “Mulole kuti Abisagi Msunamu uja apatsidwe kwa Adoniya mbale wanu, kuti akhale mkazi wake.” Mfumu Solomoni adafunsa mai wakeyo kuti, “Chifukwa chiyani mukumpemphera Abisagi Msunamu Adoniyayu? Mpemphereninso ndi ufumu womwe, poti iyeyu ndi mkulu wanga, ndipo akugwirizana ndi wansembe Abiyatara ndiponso Yowabu mwana wa Zeruya.” Pomwepo mfumu Solomoni adalumbira m'dzina la Chauta kuti, “Mulungu andilange koopsa ngati Adoniya saphedwa chifukwa cha zimenezi. Nchifukwa chake, pali Chauta wamoyo, amene adandisankhula ndi kundikhazika pa mpando waufumu wa Davide bambo wanga, nandipatsa ufumuwu monga momwe adalonjezera, Adoniya aphedwa ndithu lero lomwe lino.” Choncho mfumu Solomoni adatuma Benaya mwana wa Yehoyada, ndipo iye adakamkantha Adoniyayo, naafa. Tsono mfumu idauza wansembe Abiyatara kuti, “Pita ku Anatoti ku minda yako. Uyenera kufa ndithu, koma sindikupha tsopano lino ai, chifukwa udasunga Bokosi lachipangano la Chauta pamaso pa Davide bambo wanga, ndiponso poti udazunzika naye limodzi bambo wanga.” Choncho Solomoni adachotsa Abiyatara pa ntchito yokhala wansembe wa Chauta. Motero zidachitikadi zija adaanena Chautazi za banja la Eli ku Silo. Pamene Yowabu adamva zimenezi, adathaŵira ku hema lopatulika la Chauta nakagwira nsonga za guwa lansembe. Yowabu ndiye uja ankathandiza Adoniya koma osati Abisalomu. Tsono Mfumu Solomoni atamva kuti Yowabu wathaŵira ku hema la Chauta, ndipo kuti wakhala pambali pa guwa lansembe, adatuma Benaya mwana wa Yehoyada namuuza kuti, “Pita, ukamuphe.” Choncho Benaya adapita ku hema la Chauta lija, ndipo adauza Yowabuyo kuti, “Mfumu ikukulamula kuti utuluke.” Koma Yowabuyo adati, “Iyai, ine ndifera pompano.” Apo Benaya adakauzanso mfumu zimene Yowabu adaanena. Mfumu idamuyankha kuti, “Kachite monga momwe iye waneneramo. Ukamuphe, ndipo ukamuike m'manda. Motero udzandichotsera ine pamodzi ndi banja la bambo wanga mlandu wa imfa ya anthu amene Yowabu adaŵapha popanda chifukwa. Chauta adzambwezera ntchito zake zokhetsa magazi chifukwa choti iye adapha ndi lupanga anthu abwino aŵiri aja amene anali osalakwa kupambana iyeyo, bambo wanga Davide osadziŵa. Anthu aŵiriwo ndiwo Abinere mwana wa Nere ndi mtsogoleri wa ankhondo a ku Israele, ndiponso Amasa mwana wa Yetere mtsogoleri wa ankhondo a ku Yuda. Choncho chilango cha magazi omwe adakhetsa aja chibwerere pa Yowabu ndiponso pa zidzukulu zake mpaka muyaya. Koma mtendere wochokera kwa Chauta ukhale pa Davide ndi zidzukulu zake, pa banja lake ndi pa mpando wake waufumu, mpaka muyaya.” Pamenepo Benaya mwana wa Yehoyada adapita nakamkantha Yowabu, nkumupha, ndipo adamuika m'manda ku nyumba yake ku chipululu. Tsono mfumu idaika Benaya mwana wa Yehoyada kuti aziyang'anira gulu lankhondo m'malo mwa Yowabu, ndipo idaika wansembe Zadoki m'malo mwa Abiyatara. Pambuyo pake mfumu idatuma anthu kukaitana Simei, ndipo atabwera, idamuuza kuti, “Umange nyumba yako muno mu Yerusalemu, ndipo uzikhala mommuno, osamatuluka kukayenda kwina kulikonse. Ukadzatuluka ndi kuwoloka mtsinje wa Kidroni, mosapeneka konse udzaphedwa. Magazi ako adzakhala pamutu pako.” Simei adauza mfumu kuti, “Zimene mukunenazi nzabwino. Ine kapolo wanu ndidzachita monga momwe mwaneneramu, mbuyanga mfumu.” Choncho Simei adakhala mu Yerusalemu masiku ambiri. Koma zidangotere kuti patapita zaka zitatu, akapolo aŵiri a Simei adaathaŵira kwa Akisi, mwana wa Maaka, mfumu ya ku Gati. Simei atamva kuti akapolo ake ali ku Gati, adanyamuka pa bulu, napita ku Gati kwa Akisi, kukafunafuna akapolo ake. Simeiyo adapita, ndipo adakaŵatenga akapolo ake aja ku Gati. Tsono Solomoni atamva kuti Simei adaapita ku Gati kuchoka ku Yerusalemu, ndipo kuti adabwerako, adamuitanitsa Simeiyo namufunsa kuti, “Kodi sindidakulumbiritse iwe m'dzina la Chauta ndi kukuchenjeza kwathunthu kuti tsiku limene udzatuluke ndi kupita kwina kulikonse, udzaphedwa? Ndipo iwe udaandiwuza kuti, ‘Zimene mwanenazi nzabwino, ndimvera.’ Nanga chifukwa chiyani tsono sudasunge zimene udalumbira kwa Chauta, ndiponso sudasunge lamulo limene ndidakulamula?” Mfumu idauzanso Simei kuti, “Ukudziŵa mumtima mwakomo zoipa zonse zimene udamchita Davide, bambo wanga. Tsopano Chauta akubwezera zoipa zako pa iwe. Koma Chauta adzandidalitsa ine mfumu Solomoni, ndipo mpando waufumu wa Davide adzaukhazikitsa mpaka muyaya.” Pamenepo mfumuyo idalamula Benaya mwana wa Yehoyada. Ndipo iye adatuluka nakamupha Simeiyo. Motero ufumu wa Solomoni udakhazikikadi. Solomoni adapalana chibwenzi ndi Farao mfumu ya ku Ejipito pokwatira mwana wa Faraoyo. Adabwera naye mkaziyo ku mzinda wa Davide ku Yerusalemu, nakhala naye komweko mpaka atamaliza kumanga nyumba yake yatsopano ndi Nyumba ya Chauta ndiponso linga lozungulira mzindawo. Anthu nsembe ankatsirirabe ku akachisi osiyanasiyana, chifukwa choti nthaŵi imeneyo anali asanammangire nyumba Chauta. Solomoni ankakonda Chauta, namasunga malamulo a Davide bambo wake. Komabe ankapereka nsembe ndi kufukiza lubani ku akachisi aja. Nthaŵi ina mfumu idapita ku Gibiyoni kukapereka nsembe, popeza kuti kumeneko ndiko kunali kachisi woposa ena. Solomoni ankapereka nsembe zopsereza pa guwa limenelo zokwanira 1,000. Ku Gibiyoniko Chauta adamuwonekera Solomoni m'maloto usiku, namuuza kuti, “Upemphe chilichonse chimene ufuna kuti ndikupatse.” Solomoni adati, “Inu Mulungu, mudaonetsa chikondi chanu chachikulu ndi chosasinthika kwa mtumiki wanu Davide, bambo wanga, chifukwa choti ankachita zokhulupirika ndi zolungama, ndipo ankayenda moongoka mtima pamaso panu. Ndipo mudamuwonetsabe chikondi chachikulu ndi chosasinthikacho, pakumpatsa mwana amene wakhala pa mpando waufumu wake masiku ano. “Tsopano, Inu Chauta Mulungu wanga, mwaika mtumiki wanune pa malo a Davide bambo wanga, ngakhale ndine mwana wamng'ono chabe, ndipo sindidziŵa kagwiridwe kake ka ntchito yanga. Tsono ine mtumiki wanu ndikukhala pakati pa anthu amene mudaŵasankha, mtundu waukulu, anthu ake ochuluka, oti nkosatheka kuŵaŵerenga. Nchifukwa chake mundipatse mtumiki wanune nzeru zolamulira anthu anu, kuti ndizidziŵa kusiyanitsa zabwino ndi zoipa. Nanga popanda nzeruzo ndani angathe kulamulira mtundu waukulu chotere wa anthu anu?” Zidaŵakomera Ambuye kuti Solomoni adapempha zimenezi. Tsono Mulungu adauza Solomoni kuti, “Chifukwa chakuti wapempha zimenezi, osapempha moyo wautali kapena chuma kapena imfa ya adani ako, koma nzeru zolamulira anthu bwino, ndiye Ine ndikuchitira zimene wapempha. Zoona, ndikupatsa mtima wanzeru ndi waluntha, kotero kuti sadaonekepo nkale lonse wina wofanafana nawe, ndipo sadzaonekanso wina wolingana nawe, iweyo utafa. Kuwonjezera pamenepo, ndikukupatsanso zimene sudapemphe: chuma ndi ulemu, kotero kuti palibe mfumu imene idzalingane nawe pa masiku onse a moyo wako. Ndipo ukamadzandimvera ndi kumasunga malamulo anga, monga momwe ankachitira bambo wako Davide, udzakhala ndi moyo wautali kwabasi.” Solomoni adadzuka nazindikira kuti anali maloto. Adabwerera ku Yerusalemu, nakaimirira patsogolo pa Bokosi lachipangano la Chauta. Kumeneko adapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, kenaka adakonzera nduna zake zonse phwando. Tsiku lina akazi aŵiri adama adadza kwa Solomoni naimirira pamaso pake. Mkazi woyamba adati, “Inu mbuyanga, ine ndi mnzangayu timakhala nyumba imodzi. Tsono ine ndidaona mwana, mnzangayu ali m'nyumba momwemo. Tsiku lachitatu lake, ine nditachira kale, mnzangayu nayenso adaona mwana. Ndipo ifeyo tinali tokha, panalibe munthu wina aliyense m'nyumbamo, koma aŵiri tokhafe. Koma mwana wa mnzangayu adafa usiku, chifukwa adaamugonera. Tsono iyeyu adadzuka pakati pa usiku, natenga mwana wanga kumimba kwanga namgoneka kumimba kwake, ndipo adagoneka mwana wake wakufayo kumimba kwanga. Nthaŵiyo nkuti mdzakazi wanune ndili m'tulo. M'maŵa nditadzuka kuti ndiyamwitse mwana wanga, ndidaona kuti ngwakufa. Koma nditayang'anitsitsa, ndidaona kuti si mwana wanga ai.” Koma mkazi wina uja adamdula pakamwa nati, “Iyai, mwana wamoyoyu ndiye wanga, wako ndi wakufayu.” Mkazi woyamba uja adati, “Iyai, mwana wakufayu ngwako, koma wamoyoyu ngwanga.” Adaatero kulankhula kwake azimaiwo pamaso pa mfumu. Tsono mfumu idati, “Wina akuti, ‘Mwana wamoyoyu ngwanga,’ winanso akuti, ‘Iyai, mwana wako ngwakufayu, wanga ngwamoyoyu.’ ” Ndiye mfumuyo idati, “Patseni lupanga.” Adabwera nalo lupanga kwa mfumu. Tsono mfumu idagamula kuti, “Mduleni pakati mwana wamoyoyu, aliyense mwa azimai aŵiriŵa mumpatse chigawo chimodzi.” Pomwepo mai amene anali mwini wake wa mwana wamoyoyo adagwidwa ndi chisoni chachikulu mu mtima chifukwa cha mwanayo. Choncho adauza mfumuyo kuti, “Pepani, mbuyanga, ingompatsani iyeyu mwana wamoyoyu, musamuphe, ndakupembani.” Koma mai wina uja adati, “Iyai asapatse ine kapena iwe, amdule pakati basi!” Tsono mfumu idayankha kuti, “Perekani mwana wamoyoyu kwa mai woyamba uja, musamuphe ai. Ameneyu ndiye mai wake wa mwanayu.” Ndipo Aisraele onse adamva za m'mene mfumu idagamulira mlanduwo. Motero anthu adayamba kulemekeza Solomoni, chifukwa adaona kuti anali ndi nzeru za Mulungu zoweruza mwachilungamo. Mfumu Solomoni ankalamulira dziko lonse la Israele, ndipo nduna zake zikuluzikulu zinali izi: Azariya mwana wa Zadoki anali wansembe. Elihorefe ndi Ahiya ana a Sisa, anali alembi. Yehosafati mwana wa Ahiludi anali wolemba mbiri. Benaya mwana wa Yehoyada anali mtsogoleri wankhondo. Zadoki ndi Abiyatara anali ansembe. Azariya mwana wa Natani ankayang'anira nduna zam'zigawo. Zabudi mwana wa Natani anali wansembe ndi mlangizi wapadera wa mfumu. Ahisara anali mkulu woyang'anira nyumba ya mfumu. Ndipo Adoniramu, mwana wa Abida, anali mkulu woyang'anira ntchito zathangata. Solomoni anali ndi nduna khumi ndi ziŵiri zimene adaziika m'zigawo zonse za dziko la Israele. Nduna zimenezi zinkapereka chakudya kwa mfumu ndi banja lake lonse. Nduna iliyonse inkapereka chakudya mwezi umodzi pa chaka. Maina ndi aŵa: Benihuri, ku dziko lamapiri la Efuremu. Benedekere ku mizinda iyi: Makazi, Salabimu, Betesemesi, Etoni ndi Betehanani. Benihesedi ankayang'anira ku mzinda wa Aruboti. Ankayang'aniranso Soko ndi dziko lonse la Hefere. Benabidanabu ankayang'anira dziko lonse la mapiri la Dori. Iyeyo anali atakwatira Tafati mwana wa Solomoni. Baana mwana wa Ahiludi ankayang'anira ku Tanaki, Megido ndi ku Beteseani konse, pafupi ndi Zaretani kunsi kwake kwa Yezireele, ndiponso kuyambira ku Beteseani mpaka ku Abele-Mehola kukafika mpaka ku Yokomeamu. Benigebere ankayang'anira ku Ramoti-Giliyadi ndi midzi ya Yairo mwana wa Manase, imene ili ku Giliyadi. Analinso ndi chigawo cha Aigobu, chimene chili ku Basani, mizinda yaikulu 60 yokhala ndi malinga ndiponso zitseko zamkuŵa. Abinadabu mwana wa Ido ankayang'anira ku Mahanaimu. Ahimaazi ankayang'anira ku Nafutali. Iyeyu adaakwatira Basemati mwana wa Solomoni. Baana, mwana wa Husai ankayang'anira ku Asere ndi ku Bealoti. Yehosafati, mwana wa Paruwa, ankayang'anira ku Isakara. Simei mwana wa Ela ankayang'anira ku Benjamini. Gebere, mwana wa Uri, ankayang'anira ku dziko la Giliyadi kuphatikizapo dziko limene lidaali la Sihoni mfumu ya Aamori, ndiponso la Ogi mfumu ya ku Basani. Panalinso nduna yaikulu imodzi yoyang'anira dziko lonse la Yuda. Ayuda ndi Aisraele anali ochuluka ngati mchenga wa m'mbali mwa nyanja. Anali okondwa chifukwa anali ndi zakudya ndi zakumwa zambiri. Solomoni ankalamulira maiko onse kuyambira ku mtsinje wa Yufurate mpaka ku dziko la Afilisti, kukafika mpaka ku malire a Ejipito. Maikowo ankakhoma msonkho ndi kumatumikira Solomoni pa masiku onse a moyo wake. Chakudya chofunika ku nyumba ya mfumu pa tsiku limodzi chinkakwanira madengu 150 a ufa wosalala ndi madengu 300 a mgaiwa, ng'ombe khumi zonenepa zodyetsera m'khola, ng'ombe zakubusa makumi aŵiri, nkhosa 100, osaŵerengera ngondo, nswala, mphoyo ndiponso mbalame zonona zoŵeta. Solomoni ankalamulira dziko lonse la kuzambwe kwa mtsinje wa Yufurate, kuyambira ku Tifisa mpaka ku Gaza. Mafumu onse akumeneko adamgonjera, choncho Solomoni anali pamtendere ndi maiko ozungulira. Choncho nthaŵi yonse Solomoni ali moyo anthu a ku Yuda ndi a ku Israele anali paufulu, kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba. Munthu aliyense ankangodzikhalira pamtendere, osasoŵa kanthu kalikonse. Ndipo Solomoni anali ndi zipinda 40,000 zosungiramo akavalo okoka magareta ake, analinso ndi anthu 12,000 okwera pa akavalo. Tsono nduna khumi ndi ziŵiri zija zinkapereka chakudya cha mfumu Solomoni ndi cha anthu onse amene ankadzadya nao kunyumba kwa mfumu, nduna iliyonse mwezi wake. Ndunazo sizinkalola kuti kanthu kalikonse kasoŵe. Barele nayenso ndi udzu wodyetsa akavalo okoka magareta ndiponso akavalo enanso, zonsezo ankabwera nazo kumalo kumene zinkafunika, nduna iliyonse monga m'mene ankaiwuzira. Mulungu adapatsa Solomoni nzeru ndi luntha losaneneka, nzeru zake zinali zopanda malire. Motero nzeru za Solomoni zidapambaniratu nzeru za anthu onse akuvuma, ndiponso za anthu onse a ku Ejipito. Iyeyo anali wanzeru kuposa anthu ena onse, kuposa ngakhale Etani wa ku Ezara, kuposanso Hemani, Kalikoli ndi Darida, ana a Maholi. Ndipo mbiri yake idamveka kwa anthu a mitundu yonse yozungulira dziko lake. Solomoniyo adapeka miyambi 3,000, ndiponso nyimbo zokwanira 1,005. Ankaphunzitsa za mitengo, kuyambira mkungudza wa ku Lebanoni mpaka kachitsamba ka hisope komera pa khoma. Ankaphunzitsanso za nyama, mbalame, zinthu zokwawa pansi ndiponso za nsomba. Motero anthu ankabwera kwa Solomoni kuchokera ku maiko onse, kuti adzamve nzeru zake. Ankatumizidwa ndi mafumu onse a pa dziko lapansi amene anali atamva mbiri ya nzeru zake. Tsono Hiramu mfumu ya ku Tiro adatuma akazembe ake kwa Solomoni, atamva kuti adamdzoza ufumu m'malo mwa bambo wake, poti Hiramuyo ankakondana ndi Davide nthaŵi zonse. Ndipo Solomoni adabweza mau kwa Hiramu akuti, “Mukudziŵa kuti Davide, bambo wanga, sadathe kumangira nyumba Chauta Mulungu wake, chifukwa cha nkhondo zomwe adani ake adaamzinga nazo mbali zonse. Koma potsiriza Chauta adapereka adani akewo mu ulamuliro wake. Tsopano Chauta Mulungu wanga wandipatsa mtendere mbali zonse za dziko, kotero kuti ndilibe mdani kapena chovuta chilichonse. Choncho ndikufuna kumangira nyumba Chauta Mulungu wanga, monga momwe Iye adaauzira bambo wanga Davide kuti, ‘Mwana wako amene ndidzamukhazike pa mpando wako waufumu m'malo mwako, ndiye amene adzandimangire nyumba.’ Nchifukwa chake tsono, mulamule anthu anu kuti andidulire mikungudza ya ku Lebanoni. Tsono anthu anga adzagwira ntchito pamodzi ndi anthu anuwo, ndipo ine ndidzakulipirani chifukwa cha anthu anu malipiro amene mungatchule. Inu mukudziŵa kuti pakati pathupa, palibe munthu wodziŵa kudula mitengo ngati Asidoni.” Tsono Hiramu atamva mau a Solomoniwo, adakondwa kwambiri, ndipo adati, “Lero Chauta atamandike chifukwa adapatsa Davide mwana wanzeru kuti alamulire mtundu wotchukawu.” Ndipo adabweza mau kwa Solomoni akuti, “Ndamva zimene mwandipempha. Ndili wokonzeka kuchita zonse zimene mukufunazo, zoti anthu anga akudulireni mitengo ya mkungudza ndi ya paini. Anthu anga adzatsika nayo kuchokera kuno ku Lebanoni mpaka ku nyanja. Ndipo adzaiyandamitsa pa madzi pa phaka, kuti apite nayo ku malo amene munene. Tsono adzaimasulira kumeneko, ndipo inu mudzailandira. Chofuna ine nchongoti inuyo mudzandipatse chakudya chodyetsa anthu anga.” Choncho Hiramu adapereka kwa Solomoni mitengo yonse ya mkungudza ndi ya paini imene ankakhumbayo. Ndipo Solomoni adapatsa Hiramu tirigu wokwanira mitanga 20,000 kuti akhale chakudya cha anthu ake, ndiponso mafuta oyenga bwino okwanira mbiya zikuluzikulu 20,000. Ankapereka zimenezi kwa Hiramu chaka ndi chaka. Tsono Chauta adampatsa Solomoni nzeru monga momwe adaalonjezera. Choncho panali mtendere pakati pa Hiramu ndi Solomoni, ndipo aŵiriwo adachita chipangano cha ubwenzi. Mfumu Solomoni adayambitsa ntchito yathangata m'dziko lonse la Israele. Ndipo anthu athangatawo analipo 30,000. Ankaŵatuma ku Lebanoni anthu 10,000 pamwezi, mosinthanasinthana. Ku Lebanoni ankakhalako mwezi umodzi, ndipo kwao ankakhalako miyezi iŵiri. Adoniramu ndiye amene ankayang'anira ntchito yathangatayo. Solomoni analinso ndi anthu amtengatenga 70,000, ndi anthu 80,000 osema miyala ku dziko lamapiri. Analinso ndi akapitao 3,300 amene ankayang'anira anthu ogwira ntchito. Mfumu idalamula kuti anthuwo akumbe ndi kusema miyala ikuluikulu yabwino kwabasi, yoti akamangire maziko a Nyumba ya Chauta. Amisiri omanga a Solomoni, pamodzi ndi a Hiramu, ndiponso anthu a ku Gebala, ndiwo amene ankasema miyala, ndi kukonza mitengo ndi miyala yomangira Nyumbayo. Pakutha pa zaka 480 Aisraele atatuluka ku Ejipito, chaka chachinai cha ufumu wa Solomoni wolamulira Aisraele, pa mwezi wa Zivi, umene uli mwezi wachiŵiri, Solomoni adayambapo kumanga Nyumba ya Chauta. Nyumba imene mfumu Solomoni adamangira Chauta muutali mwake inali ya mamita 27, muufupi mwake inali ya mamita asanu ndi anai, ndipo msinkhu wake unali wa mamita pafupi 13 ndi theka. Tsono chipinda chakubwalo m'mimba mwake munali mwa mamita asanu ndi anai, kulingana ndi muufupi mwa Nyumbayo. Kutalika kunali kwa mamita anai ndi theka. Adaika mawindo amene mafuremu ake anali oloŵa m'kati mwa makoma. Adamanganso zipinda zosanjikizana pafupi ndi khoma la Nyumba, kuzungulira makoma a Nyumba yaikuluyo ndi a malo opatulika a m'kati. Chipinda chapansi m'mimba mwake chinali ngati mamita aŵiri, ndipo chipinda chapakati m'mimba mwake chinali ngati mamita aŵiri ndi theka. Chipinda cha pamwamba penipeni m'mimba mwake chinali mamita atatu. Kunja, pa makomawo adamangapo nsolomondo kuzungulira Nyumbayo, kuti asamapise mitanda m'makoma a Nyumbayo. Nyumbayo poimanga, idamangidwa ndi miyala yosemeratu. Choncho pogwira ntchitoyo, sipadamveke nyundo, nkhwangwa kapena chipangizo chilichonse chachitsulo. Chipata choloŵera ku chipinda chapansi chija chinali chakumwera kwa Nyumbayo. Anthu ankachita kukwera makwerero pochoka ku chipinda chapansi kupita ku chipinda chapakati, chimodzimodzi pochoka ku chipinda chapakati kupita ku chipinda chapamwamba. Choncho adamanga Nyumbayo mpaka kuimaliza. Ndipo siling'i yake ya Nyumbayo adaipanga ndi mitanda ndi matabwa amkungudza. Adatsirizanso zipinda zosanjikana kuzungulira Nyumbayo. Chipinda chilichonse msinkhu wake unali ngati mamita aŵiri, ndipo adazilumikiza ku Nyumbayo ndi mitanda yamkungudza. Tsono Chauta adauza Solomoni kuti, “Kunena za Nyumba ukumangayi, iwe ukamamvera mau anga ndi malangizo anga ndi kutsata malamulo anga onse, Ine ndidzakuchitiradi zimene ndidalonjeza kwa Davide bambo wako. Ndiye kuti Ine ndidzakhala pakati pa Aisraele, Aisraele anthu anga sindidzaŵasiya.” Choncho Solomoni adamanga Nyumba ya Chauta naimaliza. Pambuyo pake makoma a Nyumba ya Chauta m'kati mwake Solomoni adaŵachinga ndi matabwa amkungudza, kuyambira pansi pa Nyumbayo mpaka ku siling'i. Pansi pake pa Nyumbayo adayalapo matabwa apaini. Kumbuyo kwa Nyumbayo adadula chipinda kutalika kwake mamita asanu ndi anai. Adachimanga ndi matabwa amkungudza kuyambira pansi mpaka ku siling'i. Chipindachi adachimanga m'kati mwa Nyumbayo, kuti chikhale chipinda chopatulika cham'kati, malo opatulika kopambana. Chigawo cha Nyumba chimene chinali patsogolo pa chipinda chopatulikacho, m'litali mwake chinali mamita 18. M'kati mwa Nyumbayo pa matabwa amkungudza aja adajambulapo zithunzi za zikho ndi za maluŵa. Ponse panali mkungudza wokhawokha, miyala ya khoma osaoneka. Chipinda chopatulika chija adachikonza m'kati mwenimweni mwa Nyumbayo, kuti aikemo Bokosi lachipangano la Chauta. Chinali cha mamita asanu ndi anai ponseponse, m'litali mwake, m'mimba mwake ndiponso mumsinkhu mwake. Ndipo adachikuta ndi golide weniweni. Adapanganso guwa lansembe la matabwa amkungudza. Tsono Solomoni adakuta golide weniweni m'kati mwake mwa Nyumbayo, ndipo adalambalika maunyolo agolide mopingasitsa kutsogolo kwa chipinda chopatulika cham'kati naŵakuta ndi golide. Chipinda chimenechinso chidakutidwa ndi golide. Motero adaikuta Nyumba yonseyo ndi golide mpaka idatha. Guwa lansembe la m'chipinda chopatulika nalonso adalikuta ndi golide. Adapanga akerubi aŵiri a mtengo wa olivi, msinkhu wa aliyense unali mamita anai ndi theka, ndipo adaŵaika m'chipinda chopatulika cham'kati chija. Phiko limodzi la kerubi kutalika kwake kunali mamita aŵiri nkanthu, phiko linanso kutalika kwake mamita aŵiri nkanthu. Kufunyulula mapiko aŵiriwo, kuchokera nsonga ina mpaka nsonga ina, kutalika kwake kunali mamita anai ndi theka. Kerubi winayo msinkhu wake unalinso mamita anai ndi theka. Akerubi aŵiri onsewo anali a misinkhu yofanana ndi a mapangidwe ofanananso. Kerubi mmodzi msinkhu wake unali mamita anai ndi theka, kerubi winayo analinso chimodzimodzi. Solomoni adaika akerubiwo m'chipinda cha m'kati mwenimweni mwa Nyumbayo. Ndipo mapiko ao adaŵatambalitsa kotero kuti phiko limodzi la kerubi mmodzi linkakhudza khoma lina, ndipo phiko limodzinso la kerubi winayo linkakhudza khoma lina. Mapiko enawo ankakhudzana pakati pa Nyumba. Ndipo akerubiwo adaŵakuta ndi golide. Adazokota zithunzi za akerubi, mitengo ya mgwalangwa ndi maluŵa, kuzungulira makoma onse a Nyumbayo, ndiponso m'zipinda zam'kati ndi zakunja zomwe. Kenaka adayalanso golide pansi m'Nyumbamo m'zipinda zam'kati ndi zakunja zomwe. Ndipo adapanga zitseko za mtengo wa olivi zoloŵera ku chipinda chopatulika chija. Lentulo pamodzi ndi mphuthu zake zinali ndi mbali zisanu. Pa zitseko ziŵiri zija za mtengo wa olivi adazokotapo zithunzi za akerubi, za mitengo ya mgwalangwa ndi maluŵa. Tsono zitsekozo adazikuta ndi golide, ndipo adapaka golide pa akerubiwo ndi pa mitengo ya mgwalangwa ija. Adapanganso chimodzimodzi mphuthu za mtengo wa olivi za pa khomo la Nyumbayo, zokhala ndi mbali zinai. Ndipo adapanga zitseko ziŵiri za mtengo wa paini. Zigawo ziŵiri za chitseko chimodzi zinali zotha kupindapinda, zigawo ziŵiri za chitseko china zinalinso zotha kupindapinda. Pa zitsekopo adazokotapo akerubi, mitengo ya mgwalangwa ndiponso maluŵa. Ndipo zozokotazo adazikuta ndi golide wopsapsalala. Adamanganso bwalo lam'kati. Makoma ake adapanga ndi miyala yosema mizere itatu, mosinthanitsana ndi mzere umodzi wa matabwa amkungudza. Maziko a Nyumba ya Chauta adamangidwa pa chaka chachinai, mwezi wa Zivi. Tsono pa chaka cha 11 mwezi wa Buli, mwezi wachisanu ndi chitatu, madera onse a Nyumbayo adatha kumangidwa monga momwe kunkafunikira. Nyumbayo adaimanga pa zaka zisanu ndi ziŵiri. Solomoni adatha zaka khumi ndi zitatu akumanga nyumba yake yachifumu, ndipo adaimariza nyumba yonseyo. Nyumbayo inali ndi chigawo china chachikulu chotchedwa Nyumba ya Nkhalango ya ku Lebanoni. M'litali mwake inali mamita 44, m'mimba mwake inali mamita 22, msinkhu wake unali mamita 13 ndi theka. Adaimanga pamwamba pa mizere inai ya nsanamira zamkungudza, ndipo panali mitanda yamkungudza pamwamba pa nsanamirazo. Pamwamba pa mitandapo panali matabwa amkungudza okuta zipinda zimene zidaamangidwa pa nsanamira 45, pa mzere uliwonse nsanamira khumi ndi zisanu. Panalinso mafuremu a mawindo mizere itatu, windo kupenyana ndi windo linzake. Mawindowo ankapenyana atatuatatu. Ndipo makomo onse ndi mawindo omwe, mafuremu ake anali olingana monsemonse, m'litali mwake ndi m'mimba mwake, ndipo windo linkapenyana ndi windo linzake pa mizere itatu. Panali chigawo chinanso chachikulu chotchedwa Holo ya Nsanamira. M'litali mwake inali ya mamita 22, m'mimba mwake inali ya mamita 13 ndi hafu. Patsogolo pake panali kakhonde ka nsanamira kokhala ndi denga lake. Adamanganso chigawo china chachikulu chotchedwa Holo ya Mpando Wachifumu, kapena Holo ya Chiweruzo, modzaweruzira milandu. M'kati mwake adaikuta ndi matabwa amkungudza kuyambira pansi mpaka ku siling'i. Tsono nyumba yakeyake kumene ankayenera kukakhalako, adaimanga ku bwalo lina, kumbuyo kwa holo imeneyo. Adaimanga chimodzimodzi ngati holoyo. Ndipo adamanganso chigawo china chofanana ndi holo ya Mpando wachifumu ija kumangira mkazi wake, mwana wa Farao. Zonsezi zidamangidwa ndi miyala yabwino kwambiri imene adaisema potsata miyeso yake yofunika, yochekedwa ndi sowo m'kati ndi kunja komwe. Miyala yotere adamangira nyumba kuchokera pa maziko mpaka pamwamba pa khoma, kuyambiranso m'bwalo la Nyumba ya Chauta mpaka ku bwalo lalikulu. Mazikowo adamangidwa ndi miyala yabwino kwambiri, yaikulu bwino, kutalika kwake inali mamita atatu ndi theka, ina mamita anai. Ndipo pamwamba pake panalinso miyala yabwino kwambiri yosemedwa potsata miyeso yake yofunika, ndiponso pamwamba pa miyalayo panali matabwa amkungudza. Bwalo lalikulu kuzungulira nyumbayo lidamangidwa mizere itatu yamiyala yosemedwa, ndi mzere umodzi wa mitengo yamkungudza. Bwalo lam'kati la nyumbayo ndiponso khonde lake la nyumbayo adazimanga chimodzimodzi. Tsono mfumu Solomoni adatumiza mau ku Tiro kukaitana Huramu kuti abwere. Iyeyo anali mwana wa mai wamasiye wa fuko la Nafutali, ndipo bambo wake anali wa ku Tiro, mmisiri wa mkuŵa. Huramuyo anali wanzeru kwambiri, womvetsa zinthu, ndiponso waluso popanga zinthu zilizonse zamkuŵa. Adafika kwa mfumu Solomoni, nagwira ntchito zonse za Solomoniyo. Huramu adasungunula mkuŵa, napanga nsanamira ziŵiri. Nsanamira ina msinkhu wake unali mamita asanu ndi atatu, ndipo mjintchi wake unali pafupi mamita asanu ndi theka. Nsanamirayo inali ndi mphako, ndipo kuchindikira kwake kunali ngati kuyesa zala zinai. Nsanamira inzakeyo inali chimodzimodzi. Adasungunula mkuŵa, napanganso mitu iŵiri, ndipo adaiika pamwamba pa nsanamira zija. Mutu wina kutalika kwake kunali mamita aŵiri nkanthu, ndipo winawo kutalika kwake kunalinso mamita aŵiri nkanthu. Ndipo adapanga maukonde aŵiri olukanalukana ndi oyangayanga, naŵaika pa mitu ya pa nsanamirazo. Ukonde umodzi pa mutu wina, ndiponso ukonde umodzi pa mutu winanso. Adapanganso mizere iŵiri ya zinthu zonga makangaza mozungulira pamwamba pa ukonde, kuti aphimbe mutu wa pamwamba pa nsanamira. Adachitanso chimodzimodzi ndi mutu winawo. Tsono mitu imene inali pamwamba pa nsanamira m'khonde, inali itasemedwa ngati maluŵa a kakombo, kutalika kwake pafupifupi mamita aŵiri. Mituyo inali pamwamba pa nsanamira ziŵiri zija, ndiponso pamwamba pa chigawo choulungika cha pambali pake pa ukondewo. Pa mutu umodzi panali makangaza okwanira 200 pa mizere iŵiri yozungulira, ndipo pa mutu winawo panalinso chimodzimodzi. Adaika nsanamirazo patsogolo pa khonde loloŵera ku Nyumba ya Chauta, ina chakumwera, imene adaitchula Yakini, ndipo ina chakumpoto, imene adaitchula Bowazi. Tsono pamwamba pa nsanamira zija adakongoletsapo ndi zosemasema zooneka ngati maluŵa a kakombo. Motero ntchito ya nsanamirazo idamalizika. Pambuyo pake Huramu adapanga thanki lamkuŵa. Thankilo linali loulungika. Pakamwa pake panali pa mamita anai ndi theka, kuyesa modutsa pakati pake. Msinkhu wake unali wa mamita aŵiri nkanthu ndipo kuzungulira m'thunthu mwake munali mamita 13 ndi theka. M'munsi mwa milomo yake adazokotamo tizikho kuzunguliza thunthu lonse la thankilo, ndiye kuti dera lonse la mamita 13 ndi theka. Tizikhoto tinali m'mizere iŵiri, ndipo adaatipangira kumodzi ndi thankilo pamene ankalipanga. Adalisanjika pa ng'ombe zamkuŵa khumi ndi ziŵiri. Zitatu kuyang'ana kumpoto, zitatu kuyang'ana kuzambwe, zitatu kuyang'ana kumwera, zitatu kuvuma. Thankilo linali litakhazikika pa ng'ombezo, ndipo kuti miyendo yonse yamunsi ya ng'ombezo idaaloza cham'kati. Thankilo kuchindikira kwake kunali ngati chikhatho. M'milomo mwake munkaoneka ngati m'milomo mwa chikho, ngati duŵa la kakombo. Munkaloŵa madzi okwanira malita 40,000. Tsono adapanganso maphaka khumi amkuŵa oyenda. Phaka lililonse muutali mwake linali pafupifupi mamita aŵiri, muufupi mwake linalinso pafupifupi mamita aŵiri, ndipo msinkhu wake unali mita imodzi nkanthu. Maphakawo adapangidwa motere: adapangidwa ngati matabwa amkuŵa oloŵa m'mafuremu. Ndipo pa matabwawo panali zithunzi za mikango, ng'ombe zamphongo ndi akerubi. Tsono pa mafuremuwo, pamwamba ndi pansi pake pa mikangoyo ndi ng'ombe zamphongozo, adazokotapo nkhata zamaluŵa mopendeketsa. Kuwonjezera apo, phaka lililonse linali ndi mikombero inai yamkuŵa ndiponso mitanda yake yamkuŵanso. Ndipo pa ngodya zake zinai panali zogwiriziza mbale zosambira. Popanga zogwiriziza mbalezo, m'mbali mwake adalochamo ndi nkhata zamaluŵa. Kukamwa kwake kunali kozungulira ndipo kudabzola pamwamba pa phakalo masentimita 44. Kuzama kwake kunali masentimita 18. Pakamwapo panali zozokota zokometsera. Ndipo matabwa ake anali aphanthiphanthi a mbali zofanana, osati oulungika ai. Pansi pa matabwawo panali mikombero inai. Tsono mitanda ya mikomberoyo adapangira kumodzi ndi maphakawo. Msinkhu wa mikomberoyo unali masentimita 66. Mikomberoyo idapangidwa ngati mikombero ya galeta. Mitanda yake, marimu ake, sipokosi zake ndiponso mahabu ake, zonsezo adazipanga ndi mkuŵa wosungunula. Phaka lililonse linali ndi zigwiriro zinai, chigwiriro chimodzi pa ngodya iliyonse. Zigwirirozo zidapangidwira kumodzi ndi maphakawo. Pamwamba pa phaka panali mkombero, msinkhu wake masentimita 22. Tsono pamwamba pa phakalo panalinso zogwiriziza zake ndi matabwa ake, zonsezo zinali zopangidwira kumodzi ndi phakalo. Pamwamba pa zogwiriziza zakezo ndi matabwa akewo panali zithunzi za akerubi, mikango ndiponso mitengo ya mgwalangwa, malinga ndi m'mene unaliri mpata wokwanira chilichonse. Pozungulira adalocha ndi nkhata zamaluŵa. Maphaka khumi aja adaŵapanga motero. Onsewo adapangidwa mofanana, chifukwa miyeso yake inali yolingana ndipo maonekedwe ake analinso ofanana. Pambuyo pake adapanga mbiya zikuluzikulu khumi zamkuŵa. M'mbiya iliyonse munkaloŵa madzi a malita 800, ndipo pakamwa pake panali pafupifupi mamita aŵiri, kuyesa modutsa. Maphaka khumi aja, lililonse linali ndi mbiya yake. Ndipo adaika maphaka motere: chakumwera kwa nyumbayo maphaka asanu, chakumpoto maphaka asanu. Ndipo adaika thanki lija kumwera chakuvuma. Huramu adapanganso mikhate, mafosholo ndi mabeseni. Motero Huramu adatsiriza ntchito yonse ya Nyumba ya Chauta imene ankagwirira mfumu Solomoni: ndiye kuti kumanga nsanamira ziŵiri zija, kupanga ziwaya zokutira nsonga za makapotolosi okhala pamwamba pa nsanamirazo, ndiponso maukonde aŵiri aja ophimba ziwaya ziŵiri zija za kunsonga kw makapotolosi okhala pamwamba pa nsanamirazo. Adatsirizanso kupanga makangaza 400 a maukonde aŵiri aja, mizere iŵiri ya makangaza pa ukonde uliwonse, kuphimbira ziwaya ziŵiri zija za kunsonga kwa makapotolosi okhala pamwamba pa nsanamira zija. Ndiponso adatsiriza maphaka khumi ndi mbiya khumi zija zokhala pa maphakawo, thanki lija ndi ng'ombe khumi ndi ziŵiri zosanjikapo thankilo, ndiponso mikhate ija, mafosholo ndi mabeseni aja. Ziŵiya zonsezi za m'Nyumba ya Chauta, zimene Huramu adapangira mfumu Solomoni, zidapangidwa ndi mkuŵa wonyezemira. Mfumu idapangitsa zimenezi m'chigwa cha Yordani, ku malo amtapo amene ali pakati pa Sukoti ndi Zaretani. Koma Solomoni adangozisiya ziŵiya zimenezo osaziyesa pa sikelo, chifukwa zidaalipo zambirimbiri. Motero kulemera kwa mkuŵawo sikudadziŵike. Solomoni adapangitsanso ziŵiya zimene zinali m'Nyumba ya Chauta: ndiye kuti guwa lagolide, tebulo lagolide la buledi woperekedwa kwa Mulungu, zoikaponyale za golide weniweni, kumwera zisanu, kumpoto zisanu, m'kati mwenimweni mwa malo opatulika. Adapangitsa maluŵa, nyale ndi mbano, zonse zagolide. Adapangitsanso zikho, zozimira nyale, mabeseni, mbale zofukiziramo lubani, ndiponso ziwaya zopalira moto, zonse za golide weniweni. Ndipo adapangitsa ndi golide zomangira zitseko za chipinda cham'kati mwenimweni mwa Nyumbayo, malo opatulika kopambana, ndiponso zitseko zoloŵera m'Nyumba ya Chauta. Motero Mfumu Solomoni adatsiriza ntchito zonse za ku Nyumba ya Chauta. Tsono adabwera ndi zinthu zonse zimene Davide bambo wake adaazipereka, siliva, golide, ndi ziŵiya. Adaziika m'zipinda zosungiramo chuma cha ku Nyumba ya Chauta. Pambuyo pake Solomoni adasonkhanitsa akuluakulu Aisraele, ndi atsogoleri onse a mafuko, akuluakulu a mabanja a Aisraele. Onsewo adasonkhana kwa mfumu Solomoni ku Yerusalemu, kuti akatenge Bokosi lachipangano la Chauta, kulitulutsa m'Ziyoni, mzinda wa Davide. Ndipo Aisraele onse adasonkhana pamaso pa mfumu Solomoni nthaŵi ya chikondwerero cha mwezi wa Etanimu, mwezi wachisanu ndi chiŵiri. Tsono atsogoleri onse a Aisraele atabwera, ansembe adanyamula Bokosi lachipangano lija. Adabwera nalo Bokosi la Chautalo, pamodzi ndi chihema chamsonkhano ndiponso ziŵiya zonse zopatulika zimene zinali m'chihemamo. Ansembe ndi Alevi ndiwo amene adabwera nazo zimenezo. Pamenepo mfumu Solomoni pamodzi ndi gulu lonse la Aisraele amene adaasonkhana pamaso pake, ataima patsogolo pa Bokosi lachipanganolo, ankapereka nsembe za nkhosa ndi ng'ombe zosaŵerengeka. Tsono ansembe adafika nalo ndi Bokosi lachipangano la Chauta ku malo ake a m'kati mwenimweni mwa Nyumbayo, ku malo opatulika kopambana, naliika kunsi kwa mapiko a akerubi. Choncho akerubiwo ankatambasula mapiko ao pamwamba pa Bokosilo, kotero kuti ankaliphimba pamodzi ndi mphiko zake zonyamulira. Mphikozo zinali zazitali kwambiri, kotero kuti nsonga zake zinkaonekera kukhalira ku malo opatulika, patsogolo pa malo opatulika kopambana a m'kati aja. Koma kukhalira kunja sizinkaonekera. Ndipo zili komweko mpaka pano. M'Bokosimo munalibe kanthu kena kalikonse, kupatula miyala iŵiri yokha ija imene Mose adaaikamo ku Horebu, kumene Chauta adaachita chipangano ndi Aisraele, iwowo atatuluka ku dziko la Ejipito. Tsono pamene ansembewo adatulukamo m'malo opatulikawo, mtambo udadzaza Nyumba ya Chauta. Ndipo ansembe sankatha kutumikira chifukwa cha mtambowo, pakuti ulemerero wa Chauta udaadzaza Nyumba yake ija. Tsono Solomoni adapemphera nati, “Inu Chauta mudanena kuti mudzakhala mu mdima waukulu. Koma tsopano ndakumangirani Inuyo nyumba yaulemerero, malo oti muzikhalamo mpaka muyaya.” Tsono mfumuyo idatembenukira anthu aja, nidalitsa msonkhano wonse wa Aisraele, onsewo ali chachilili. Ndipo mfumuyo idati, “Atamandike Chauta, Mulungu wa Aisraele, amene wachitadi ndi dzanja lake zimene adaalonjeza ndi pakamwa pake kwa Davide bambo wanga. Paja adaati, ‘Kuyambira tsiku limene ndidatulutsa anthu anga Aisraele ku Ejipito, sindidasankhepo mzinda pakati pa mafuko onse a Aisraele woti anthu amangeko nyumba m'mene dzina langa lizimvekamo. Koma ndidasankha Davide kuti azilamulira anthu anga Aisraele.’ Tsono maganizo adaalipo mumtima mwa bambo wanga Davide oti amange nyumba yomveketsa dzina la Chauta, Mulungu wa Aisraele. Koma Chautayo adauza Davide bambo wanga kuti, ‘Popeza unkaganiza mumtima mwako zoti undimangire nyumba, udachita bwino kumaganiza zimenezo. Komabe si ndiwe udzamange nyumbayo, koma mwana wako amene udzabale, ndiye amene adzandimangire nyumba yomveketsa dzina langa.’ Tsopano Chauta wachitadi zimene adaalonjeza zija. Pakuti ine ndi amene ndaloŵa ufumu m'malo mwa Davide bambo wanga, ndipo ndikulamulira Aisraele pa mpando wa bambo wanga, monga momwe Chauta adaalonjezera. Ndipo ndinedi amene ndamanga Nyumba yomveketsa dzina la Chauta, Mulungu wa Aisraele. Tsono m'menemo ndalikonzera malo Bokosi lija, m'mene muli mau a chipangano cha Chauta chimene adachita ndi makolo athu, pamene adaŵatulutsa ku Ejipito.” Pambuyo pake Solomoni adaimirira patsogolo pa guwa la Chauta, msonkhano wonse wa Aisraele ukuwona, ndipo adakweza manja ake kumwamba. Tsono adati, “Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, palibe Mulungu wina wonga Inu, kumwamba kapena pa dziko lapansi. Mumasunga chipangano ndi kuwonetsa chikondi chosasinthika kwa atumiki anu amene amayenda pamaso panu ndi mtimi wao wonse. Inu mwachitadi zimene mudaauza Davide bambo wanga, mtumiki wanu. Zimene zija mudaalankhula ndi pakamwa panu, dzanja lanu lazichitadi monga onse akuwoneramu lero lino. Tsono, Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, mukumbukire zimene zija mudalonjeza Davide bambo wanga, mtumiki wanu, pamene mudati, ‘Sipadzasoŵa munthu pa banja lako wokhala pamaso panga pa mpando waufumu wa dziko la Israele, malinga ana ako akamasamala mkhalidwe wao, ndi kumayenda pamaso panga anga monga momwe iweyo wayendera pamaso panga.’ Nchifukwa chake tsono, Inu Mulungu wa Aisraele, zimene mudalankhula ndi bambo wanga Davide, mtumiki wanu, zichitikedi. “Kodi Mulungu angakhale nawodi pa dziko lapansi? Onani, kumwamba ndi kumwambamwamba komwe sikukukwanirani kukhala, nanji tsono nyumba imene ndakumangiraniyi! Komabe Inu Chauta, Mulungu wanga, imvani pemphero la ine mtumiki wanu ndi kupemba kwanga. Mverani kulira kwanga ndiponso pemphero limene ine mtumiki wanu ndikupemphera pamaso panu lero lino. Usana ndi usiku maso anu azikhala otsekuka kuyang'ana Nyumba imeneyi, malo amene Inu mudanena kuti, ‘Dzina langa lidzamveka m'menemo.’ Imvani pemphero lopemba la mtumiki wanu ndiponso la anthu anu Aisraele, pamene akupemphera ku malo ano. Ndithu mumve kumwambako kumene mumakhala, ndipo mukamva, mukhululuke. “Tsono munthu akachimwira mnzake, nauzidwa kuti alumbire, akabwera kudzalumbira patsogolo pa guwa lanu m'Nyumba muno, pamenepo Inu mumve kumwambako, ndipo muchitepo kanthu ndi kuŵaweruza atumiki anuwo. Wochimwa mugamule kuti ngwolakwa ndipo mumlange molingana ndi zolakwa zakezo. Koma wosachimwayo mugamule kuti ngwopanda mlandu, ndipo mumpatse mphotho zoyenera makhalidwe akewo. “Anthu anu Aisraele atagonjetsedwa ndi adani ao chifukwa chakuti adakuchimwirani, pambuyo pake nkubwerera kwa Inu ndi kutamanda dzina lanu, napemphera ndi kupemba kwa Inu m'Nyumba muno, pamenepo Inuyo mumve kumwambako, ndipo mukhululukire tchimo la anthu anu Aisraele, kenaka muŵabwezenso ku dziko limene Inu mudapatsa makolo ao. “Kumwamba kukatsekeka, mvula nkupanda kugwa chifukwa chakuti anthuwo adakuchimwirani, pambuyo pake nkupemphera choyang'ana ku malo ano ndi kutamanda dzina lanu, natembenuka nkusiya tchimo laolo Inu mukuŵazunza, pamenepo Inuyo mumve kumwambako, mukhululukire tchimo la atumiki anu, anthu anu Aisraele. Inu muziŵaphunzitsa njira yabwino yoti aziyendamo, ndipo muzigwetsa mvula pa dziko lanu limene mudapatsa anthu anu kuti likhale choloŵa chao. “Mwina mwake m'dzikomo mudzaloŵa njala, mliri, dzimbiri lapambeu kapena chinoni, dzombe kapena kapuchi. Mwina adani ao adzaŵazinga ku mzinda wao wina uliwonse. Mwina padzakhala mliri wa mtundu wina, kapena matenda a mtundu uliwonse. Tsono, chodandaula chake chingakhale chotani, wina aliyense mwa anthu anu Aisraele akapemphera mopemba, akuzindikira zovuta za mumtima mwake, natambalitsa manja choloza ku Nyumba ino, pamenepo Inuyo mumve kumwambako kumene mumakhala. Mukhululuke, ndipo muchitepo kanthu. Mumchitire aliyense potsata makhalidwe ake onse, pakuti Inu mukudziŵa mtima wake. Inu nokha ndinu amene mumadziŵa mitima ya anthu. Motero anthu anu Aisraele azikuwopani masiku onse a moyo wao, pomakhala m'dziko limene Inu mudapatsa makolo athu. “Chimodzimodzinso mwina mlendo amene sali mmodzi wa Aisraele anthu anu, adzabwera kuchokera ku dziko lakutali atamva za dzina lanu. Zoonadi anthu adzamva ndithu za dzina lanu lotchuka ndiponso za dzanja lanu lamphamvu ndi lochita zazikulu. Iyeyo akabwera kudzapemphera ku Nyumba ino, Inu mumve kumwambako kumene mumakhala, ndipo mumchitire mlendoyo zonse zimene wakupemphani. Muchite zimenezi kuti anthu a mitundu yonse ya pa dziko lapansi adziŵe dzina lanu ndipo azikumverani, monga m'mene amachitira Aisraele anthu anu, ndipo adziŵe kuti Nyumba imene ndaimangayi imadziŵika ndi dzina lanu. “Anthu anu akamapita ku nkhondo kukamenyana ndi adani ao, kulikonse kumene mungaŵatume, akapemphera kwa Inu Chauta choyang'ana ku mzinda umene Inu mudausankha ndiponso ku Nyumba imene ndakumangiraniyi, yomveketsa dzina lanu, pamenepo Inuyo mumve kumwambako pemphero lao ndi kupemba kwao ndipo muŵapambanitse. “Mwina Aisraelewo adzakuchimwirani, poti palibe munthu amene sachimwa, ndiye Inuyo nkudzaŵakwiyira ndi kuŵapereka kwa adani, kuti aŵatenge ukapolo kupita nawo ku dziko lakutali kapena lakufupi. Tsono, ali akapolo kuchilendoko, akazindikira kuchimwa kwao natembenuka mtima ndi kupemphera kwa Inu modzichepetsa m'dziko la anthu amene adaŵagwira ukapolowo, nkumanena kuti, ‘Tachimwa, tachita zosayenera, tapalamula ndithu’. Anthuwo akabwerera kwa Inu ndi nzeru zao zonse ndi mtima wao wonse, m'dziko la adani ao kumene adaŵatengera ukapolo, ndipo akapemphera kwa Inu choyang'ana ku dziko lao limene Inu mudapatsa makolo ao, ku mzinda umene Inu mudausankha ndiponso ku Nyumba imene ine ndakumangiraniyi yomveketsa dzina lanu, pamenepo Inuyo kumwambako kumene mumakhala, mumve pemphero lao ndi kupemba kwao ndipo muŵachitire zolungama. Tsono muŵakhululukire anthu anu okuchimwiraniwo, mukhululukire machimo ao onse okupandukirani. Ndipo mufeŵetse mitima ya anthu amene adaŵagwira ukapolo aja, kuti nawonso aŵachitire chifundo. Pakutitu iwoŵa ndi anthu anuanu ndi choloŵa chanu, omwe aja mudaŵatulutsa ku Ejipito kuŵachotsa m'ng'anjo ya moto. “Yang'anani mwa chikondi chanu anthu anu Aisraele pamodzi ndi mfumu yao, ndipo muzitchera khutu nthaŵi zonse pamene akupemphani kuti muŵathandize. Pakuti Inu mudaŵasiyanitsa ndi anthu onse a pa dziko lapansi, kuti akhale anthu anuanu, monga momwe Inu mudanenera kudzera mwa Mose mtumiki wanu, pamene munkatulutsa makolo athu ku Ejipito, Inu Chauta Mulungu.” Tsono Solomoni atamaliza kupemphera mopemba kwa Chauta, adadzuka ku guwa la Chauta kumene anali atagwada, manja atakweza kumwamba. Ndipo adaimirira nadalitsa msonkhano wonse wa Aisraele mokweza mau nati, “Atamandike Chauta amene adaŵapatsa mtendere anthu ake Aisraele potsata zimene adaalonjeza. Palibe mau ndi amodzi omwe amene adapita pachabe pa zinthu zonse zabwino zimene adaalonjeza, polankhula kudzera mwa Mose mtumiki wake. Chauta Mulungu wathu akhale nafe monga momwe adaakhalira ndi makolo athu. Asatisiye kapena kutitaya. Atembenuzire mitima yathu kwa Iye, kuti tiziyenda m'njira zake ndi kusunga mau ake, malamulo ake ndi malangizo ake, amene adapatsa makolo athu. Mau angaŵa amene ndanena mopemba pamaso pa Chauta, Mulungu wathu, asaŵaiŵale mauwo masana ndi usiku. Chauta Mulungu wathu alimbikitse mtumiki wakene ndiponso athandize Aisraele anthu ake, poŵapatsa zosoŵa zao zatsikunditsiku. Choncho anthu a mitundu yonse ya pa dziko lapansi adziŵe kuti Chauta ndiye Mulungu, palibenso wina. Nchifukwa chake inu Aisraele, mitima yanu ikhale yodzipereka kwathunthu kwa Mulungu wathu, ndipo mumvere bwino mau ake, ndi kutsata malamulo ake monga lero lino.” Pambuyo pake mfumu Solomoni, pamodzi ndi Aisraele onse, adapereka nsembe kwa Chauta. Solomoni adapereka nsembe zachiyanjano kwa Chauta pakupha ng'ombe 22,000 ndi nkhosa 120,000. Motero mfumu pamodzi ndi Aisraele onsewo adaipereka Nyumba ya Chauta ija. Tsiku lomwelo mfumuyo idapatulanso malo am'kati a bwalo limene linali kumaso kwa Nyumba ya Chauta. Paja kumeneko nkumene adaperekerako nsembe yopsereza, ndiponso chopereka cha chakudya, kudzanso nthuli zamafuta za nsembe zachiyanjano zija. Adaachita izi chifukwa choti guwa lamkuŵa limene linali m'malo opatulika a Chauta linali lochepa kwambiri, kotero kuti sikudatheke kuperekerapo nsembe zonse zopsereza ndi zaufa ndiponso nthuli zamafuta za nsembe zachiyanjano. Choncho nthaŵi imeneyo Solomoni adachita chikondwerero, pamodzi ndi Aisraele onse. Unali msonkhano waukulu kwambiri, kuyambira ku chipata cha Hamati mpaka ku kamtsinje ka Ejipito. Adachita chikondwerero chimenechi chopembedza Chauta Mulungu wathu, masiku asanu ndi aŵiri. Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu, Solomoni adauza anthuwo kuti azipita. Pompo anthuwo adathokoza mfumuyo, ndipo adapita kwao ndi mtima wokondwa ndi wosangalala, chifukwa cha zokoma zonse zimene Chauta adaachitira Davide mtumiki wake, ndi anthu ake Aisraele. Tsono Solomoni atamaliza kumanga Nyumba ya Chauta ndi nyumba ya mfumu, ndiponso zonse zimene iye ankafuna kuti amange, Chauta adamuwonekera kachiŵiri, monga momwe adaachitira ku Gibiyoni kuja. Ndipo Chauta adamuuza kuti, “Ndamva pemphero lako ndi kupemba kwako kumene wachita pamaso panga. Ine ndaipatula Nyumba wamangayi, ndaikamo dzina langa kuti anthu azidzandipembedzeramo mpaka muyaya. Maso anga ndi mtima wanga zidzakhala m'menemo nthaŵi zonse. Kunena za iweyo, ukamayenda pamaso panga mokhulupirika ndi molungama, monga m'mene ankayendera Davide bambo wako, ukamachita zonse zimene ndidakulamula ndi kumvera mau anga ndi malangizo anga, pamenepo, Ine ndidzaukhazikitsa mpaka muyaya mpando wako waufumu wolamulira Aisraele, monga momwe ndidalonjezera Davide bambo wako kuti, ‘Sipadzasoŵa munthu pa banja lako wokhala pa mpando waufumu wa Israele.’ Koma iwe ndi ana ako mukapatuka ndi kuleka kunditsata Ine, mukasiya malangizo ndi malamulo anga amene ndidakupatsani, nkuyamba kutumikira milungu ina ndi kumaipembedza, pamenepo ndidzaŵachotsa Aisraelewo m'dziko limene ndidaŵapatsa. Ndipo Nyumba ino imene ndaipatulira dzina langa, ndidzaichotsa pamaso panga. Motero Aisraele adzasanduka ngati mwambi ndi chisudzo chabe pakati pa anthu a mitundu yonse. Nyumba yotchuka ndi yokomayi idzasanduka bwinja, ndipo aliyense wopitapo adzadabwa nadzaimba likhweru, nkumafunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani Chauta walichita zotere dzikoli ndiponso Nyumbayi?’ Tsono azidzati, ‘Nchifukwa chakuti anthuwo adasiya Chauta Mulungu wao, amene adatulutsa makolo ao ku dziko la Ejipito, ndipo adadzifunira milungu ina namaipembedza ndi kumaitumikira. Nkuwona Chautayo waŵachita zoipa zonsezi.’ ” Ntchito yomanga Nyumba ya Chauta ndi nyumba ya mfumu idamtengera Solomoni zaka makumi aŵiri. Mfumu Hiramu wa ku Tiro ndiye ankapereka kwa Solomoni mitengo ya mkungudza, ya paini, ndiponso golide monga m'mene Solomoni ankazifunira. Ndipo mfumu Solomoni adapatsa Hiramu mizinda makumi aŵiri ya m'dziko la Galilea. Hiramu adabwera kuchokera ku Tiro kuti adzaone mizinda imene Solomoni adampatsa, koma sidamkondweretse. Nchifukwa chake adafunsa kuti, “Kodi iwe mbale wanga, monga ndi imeneyi mizinda imene wandipatsa?” Choncho imatchulidwa kuti dziko la Kabule mpaka lero lino. Hiramu anali atatumiza kwa mfumu golide woposa makilogramu 4,000. Izi ndizo zimene adachita mfumu Solomoni: adalamula anthu kuti agwire ntchito yathangata pomanga Nyumba ya Chauta, nyumba yake, linga lotchedwa Milo kudzanso khoma lozinga Yerusalemu, ndiponso mizinda ya Hazori, Megido ndi Gezere. (Farao mfumu ya ku Ejipito anali atalanda mzinda wa Gezere, nautentha. Adaapha Akanani amene ankakhala mumzindamo ndipo adaupereka kuti ukhale mphatso kwa mwana wake wamkazi, uja adaakwatiwa ndi Solomoniyu. Choncho Solomoni adachita kuumanganso mzinda wa Gezerewo). Adamanganso mizinda iyi: Betehoroni wakunsi, Baalati, ndi Tamara wakuchipululu, m'dziko la Yuda, ndiponso mizinda yonse yosungiramo chuma chake ndi magaleta ake, mizinda ya anthu ake okwera pa akavalo, ndiponso chilichonse chimene Solomoniyo ankafuna kumanga ku Yerusalemu, ku Lebanoni ndi ku maiko onse amene iye ankalamulira. Koma analipo anthu ena otsalira a mitundu yosiyanasiyana: Aamori, Ahiti, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi. Ameneŵa sanali Aisraele, ndiye kuti zidzukulu zao zotsalira m'dzikomo. Onsewo zimene Aisraele sadathe kuŵaononga kotheratu. Anthu ameneŵa Solomoni ankaŵagwiritsa ntchito yathangata, ndipo akugwirabe ntchito imeneyo mpaka lero lino. Koma Aisraele Solomoni sankaŵagwiritsa ntchito yaukapolo. Iwowo anali anthu ake ankhondo, nduna zake, atsogoleri ankhondo, olamulira ocheperapo a ankhondo, ndiponso oyang'anira magaleta ake, ndi anthu ake okwera pa akavalo. Kunali akapitao akuluakulu oyang'anira ntchito za Solomoni. Onsewo analipo 550 ndipo ankayang'anira anthu antchito. Nthaŵi imeneyo mwana wamkazi wa Farao adachoka ku mzinda wa Davide napita ku nyumba yake imene Solomoni adammangira. Pambuyo pake Solomoni adamanga linga la Milo. Solomoni ankapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano katatu pa chaka. Ankapereka nsembezo pa guwa limene adamangira Chauta, ndipo ankafukiza lubani pamaso pa Chauta. Choncho ankasamalira zokhudza Nyumbayo. Mfumu Solomoni adapanga zombo zambiri ku Eziyoni-Gebere pafupi ndi Elati, pa gombe la Nyanja Yofiira, ku dziko la Edomu. Ndipo mfumu Hiramu adatumiza zombo zake pamodzi ndi atumiki ake, ndiye kuti amalinyero odziŵa zam'nyanja, kukagwira ntchito pamodzi ndi anthu a Solomoni. Tsono amalinyerowo adapita ku Ofiri, ndipo adakatengako golide wokwanira makilogramu 14,000, nabwera naye kwa mfumu Solomoni. Mfumukazi ya ku Sheba itamva za mbiri ya Solomoni yobukitsa dzina la Chauta, idadza ku Yerusalemu kudzamuyesa ndi mafunso apatali. Idabwera ndi atumiki ambiri ndi ngamira zonyamula zokometsera zakudya, golide wambiri ndi miyala yamtengowapatali. Itafika kwa Solomoni, idamuuza zonse za kumtima kwake. Solomoni adayankha mafunso ake onse. Panalibe kanthu kalikonse kobisika kwa Solomoniyo, kamene sadathe kuimasulira mfumukaziyo. Tsono itaona nzeru zonse za Solomoni, nyumba imene adaamanga ija, chakudya cha patebulo pake, m'mene zinkakhalira nduna zake, m'mene ankasungira mwambo atumiki ake ndi zovala zao, atumiki ake operekera zakumwa, ndiponso nsembe zake zopsereza zimene ankapereka ku Nyumba ya Chauta, mfumukaziyo idangoti kukamwa pululu, kusoŵa chonena. Pamenepo idauza mfumu Solomoni kuti, “Zimene ndinkamva ndili ku dziko lakwathu, zonena za ntchito zanu ndi nzeru zanu, nzoonadi. Zimenezo sindidazikhulupirire, mpaka nditafika ndi kuziwona chamaso. Ndipotu anthu sadaandiwuze zonse, ngakhale ndi theka lomwe. Nzeru zanu ndiponso zabwino zimene muli nazo zikuposa zimene ndinkazimva. Ngodala anthu anu. Ngodala atumiki anuŵa, amene amaima pamaso panu nthaŵi zonse ndi kumamva nzeru zanu. Atamandike Chauta, Mulungu wanu, amene wakondwera nanu, nakukhazikani pa mpando waufumu wa dziko la Israele. Chifukwa choti Chauta adakonda Israele mpaka muyaya, wakuikani kuti mukhale mfumu yolamulira moyenera ndi mwachilungamo.” Itanena zimenezo mfumukaziyo idapatsa mfumu Solomoni golide wa makilogramu 4,000, zokometsera chakudya zambirimbiri, ndiponso miyala yamtengowapatali. Sikudafikenso konse zokometsera zakudya zochuluka chotere zonga zimene mfumukazi ya ku Sheba idapatsa mfumu Solomoni. Zombo za mfumu Hiramu nazonso zidabwera ndi golide wa ku Ofiri. Zidatenganso mitengo yambiri ya alimugi ndi miyala yamtengowapatali. Mitengo imeneyo mfumuyo idasemera mizati yochirikizira Nyumba ya Chauta ndi ina yochirikizira nyumba yachifumu. Adasemanso azeze ndi apangwe a anthu oimba. Panalibe mitengo yotere imene idabweranso kapena kuwonekanso mu Israele mpaka lero lino. Mfumu Solomoni adapatsa mfumukazi ya ku Sheba ija zonse zimene inkafuna, ndiponso chilichonse chimene idaapempha, osaŵerengera mphatso zachifumu zimene anali ataipatsa kale. Tsono mfumukaziyo idabwerera ku dziko lakwao pamodzi ndi atumiki ake aja. Golide amene ankabwera kwa Solomoni pa chaka chimodzi ankakwanira makilogramu 23,000, osaŵerengera amene ankabwera ndi alendo ndi anthu amalonda, ndiponso wina wochokera kwa mafumu onse a ku Arabiya, ndi kwa nduna zam'dzikomo. Mfumu Solomoni adapangitsa zishango 200 zazikulu za golide wonsansantha. M'chishango chilichonse munkaloŵa golide pafupi makilogramu asanu ndi awiri. Adapanganso zishango 300 zazing'ono za golide wonsansantha. M'chishango chilichonse munkaloŵa golide wokwanira kilogramu limodzi ndi theka. Tsono mfumu idaika zishangozo m'Nyumba ya Nkhalango ya ku Lebanoni. Mfumu idapangitsanso mpando waukulu waufumu wa minyanga yanjovu, niwukuta ndi golide wabwino kwambiri. Mpando waufumuwo unali ndi makwerero asanu ndi limodzi okafikirapo, ndipo chosamira chake unali woulungika pamwamba. Mpandowo unali ndi chosanjikapo manja uku ndi uku, ndipo zifanizo ziŵiri za mikango itaima pambali pa zosanjikapo manjazo. Panalinso mikango pa mbali zonse ziŵiri za khwerero lililonse, mikango khumi ndi iŵiri yonse pamodzi. Mpando wotere sudapezekepo mu ufumu wina uliwonse. Zikho zonse zimene mfumu Solomoni ankamwera zinali zopangidwa ndi golide. Ziŵiya zonse za ku Nyumba ya Nkhalango ya Lebanoni nazonso zinali za golide weniweni. Panalibe zasiliva popeza kuti silivayo sanali kanthu pa nthaŵi ya Solomoni. Mfumu inali ndi zombo zochokera ku Tarisisi zimene zinkayenda pa nyanja pamodzi ndi zombo za Hiramu; ndipo chaka chachitatu chilichonse zinkabwera zitanyamula golide, siliva, minyanga yanjovu, anyani ndi apusi. Motero mfumu Solomoni adapambana mafumu onse a pa dziko lonse lapansi pa chuma ndi pa nzeru. Ndipo anthu onse a pa dziko lapansi ankafunafuna kuti amuwone Solomoni ndi kumva nzeru zake zimene Mulungu adaaika mumtima mwake. Aliyense mwa iwowo ankabwera ndi mphatso zake, zinthu zasiliva ndi zagolide, zovala, zida zankhondo, zokometsera chakudya, akavalo ndi abulu. Ndipo zimenezi zinkhachitika choncho chaka ndi chaka. Choncho Solomoni adasonkhanitsa magaleta ndiponso anthu okwera pa akavalo. Magaletawo anali nawo 1,400, anthu okwera pa akavalo analipo 12,000. Adaŵakhazika ena ku mizinda yokhalako ankhondo, ena pafupi ndi mfumu ku Yerusalemu. Tsono mu Yerusalemumo mfumu idasandutsa siliva kukhala wambiri ngati miyala wamba. Adasandutsanso mikungudza kukhala wochuluka ngati mikuyu ya m'zigwa. Solomoni ankagula akavalo ku Ejipito ndi ku Kuwe. Anthu amalonda a mfumu ankalandirira akavalo ku Kuwe, atapereka ndalama. Anthuwo ankagula galeta ku Ejipito pa mtengo wa masekeli asiliva okwana 600, ndipo kavalo pa mtengo wa masekeli asiliva 150. Momwemonso mafumu onse a Ahiti ndi a ku Siriya, nawonso ankhagula zinthuzo kudzera mwa anthu amalonda omwewo. Mfumu Solomoni ankakonda akazi ambiri achilendo. Kuwonjezera pa mwana wamkazi wa Farao, adakwatiranso akazi a mitundu iyi: Amowabu, Aamoni, Aedomu, Asidoni ndi Ahiti. Akazi ameneŵa anali a mitundu ija imene Chauta adaauza Aisraele kuti, “Musadzakwatire akazi a mitundu imeneyi, ndipo amuna amitunduyo asadzakwatire akazi a mtundu wanu, poti ndithudi iwowo adzatembenuza mitima yanu, kuti muzitsata milungu yao.” Koma Solomoni ankakondabe akazi a mitundu imeneyo. Iyeyo adakwatira ana achifumu 700 ndipo anali ndi azikazi 300. Ndipo akaziwo adamsokoneza. Solomoni atakalamba, akazi akewo adamnyengerera kuti azitsata milungu yachilendo. Choncho sadatsate Chauta, Mulungu wake, ndi mtima umodzi, monga ankachitira Davide bambo wake. Solomoni ankapembedza Asitoreti, mulungu wachikazi wa Asidoni, ndiponso Milikomu, mulungu wonyansa uja wa Aamoni. Motero Solomoni adachimwira Chauta, ndipo sadatsate Chauta ndi mtima wonse, monga ankachitira Davide, bambo wake. Tsono Solomoni adamanga akachisi pa phiri la kuvuma kwa Yerusalemu, kumangira Kemosi, mulungu wonyansa wa Amowabu, ndiponso Moleki mulungu wonyansa wa Aamoni. Akazi ake onse achilendo adaŵamangira malo ofukizirapo lubani ndi operekerapo nsembe kwa milungu yao. Choncho Chauta adakwiyira Solomoni, chifukwa choti mtima wake udaasinthika ndi kusiya Chauta, Mulungu wa Aisraele, amene adamuwonekera kaŵiri konse, namulamula kuti asatsate milungu ina. Koma Solomoni sadamvere zimene Chauta adamlamulazo. Nchifukwa chake Chauta adamuuza kuti, “Popeza kuti sudasunge chipangano changa ndi malamulo anga amene ndidakulamula, ndithudi ndidzakulanda ufumu, kuuchotsa m'manja mwako, ndi kuupereka kwa mmodzi mwa atumiki ako. Koma chifukwa cha Davide bambo wako, sindidzachita zimenezi iwe uli moyo ai. Ndidzaulanda kwa mwana wako. Komabe sindidzalanda ufumu wonse. Mwana wako ndidzamsiyirako fuko limodzi, chifukwa cha Davide mtumiki wanga, ndiponso chifukwa cha mzinda wa Yerusalemu umene ndidausankha.” Tsono Chauta adamuutsira Solomoni mdani dzina lake Hadadi, wa ku Edomu. Hadadiyo anali wa banja laufumu ku Edomuko. Kale ndithu pamene Davide ankamenyana nkhondo ndi Aedomu, Yowabu mkulu wankhondo adaapita kukakwirira Aisraele ophedwa, ndipo adakapha mwamuna aliyense ku Edomuko. Yowabu ndi ankhondo ake adaakhala kumeneko miyezi isanu ndi umodzi, mpaka adapha amuna onse a ku Edomu. Koma Hadadi adaathaŵira ku Ejipito pamodzi ndi Aedomu ena, atumiki a bambo wake. Pamenepo nkuti Hadadiyo ali mwana wamng'ono. Adanyamuka ku Midiyani, napita ku Parani, ndipo adatengako amuna ena ku Paraniko, nakafika ku Ejipito kwa mfumu Farao. Farao adapatsa Hadadi ndi anthu ake nyumba ndi chakudya, namninkhanso kadziko. Tsono Farao adakomera mtima Hadadi, kotero kuti adampatsa mlamu wake kuti akhale mkazi wake. Mkaziyo anali mbale wake wa mfumukazi Tapenesi wa ku Ejipito. Tsono mkazi wa Hadadiyo adabala mwana wamwamuna dzina lake Genubati, ndipo Tapenesi adalerera Genubati ku nyumba yaufumu. Genubatiyo ankakhala m'nyumba ya Farao pamodzi ndi ana a Farao. Koma Hadadi atamva ku Ejipitoko kuti Davide adamwalira, ndiponso kuti Yowabu mtsogoleri wankhondo nayenso adafa, adauza Farao kuti, “Loleni ndichoke kuti ndipite ku dziko lakwathu.” Koma Farao adati, “Chakusoŵa nchiyani kwathu kuno kuti uziti ukufuna kupita ku dziko lakwanu?” Hadadi adauza Farao kuti, “Iyai sizimenezo, mungondilola basi kuti ndizipita.” Mulungu adautsiranso Solomoni mdani wina, dzina lake Rezoni, mwana wa Eliyada, amene anali atathaŵa kwa mbuyake Hadadezere, mfumu ya ku Zoba. Munthu ameneyu adasonkhanitsa anthu, nakhala mtsogoleri wao wa gulu la achifwamba. Izi zidachitika pamene Davide adati atagonjetsa Hadadezere, adapha ankhondo a ku Zoba. Tsono Rezoni ndi gulu lake adapita ku Damasiko, nakakhala kumeneko, ndipo anthuwo adamlonga ufumu womalamulira dziko la Siriya. Rezoni anali mdani wa Israele masiku onse a Solomoni, namamvuta Solomoniyo monga momwe Hadadi ankachitira. Winanso woukira Solomoni anali Yerobowamu, mwana wa Nebati wa fuko la Efuremu, wa ku Zereda. Anali mmodzi mwa nduna za Solomoni, amene mai wake anali Zeruya, mkazi wamasiye. Nkhani ya kuukira kwakeyo idaayenda motere: Solomoni adaamanga linga la Milo, nakonza khoma logumuka la mzinda wa Davide bambo wake. Yerobowamu anali munthu wolimba mtima, ndipo Solomoni ataona kuti mnyamatayo ngwachangu, adamuika kuti akhale kapitao woyang'anira ntchito yathangata m'dziko la ana a Yosefe. Ndiye tsiku lina pamene Yerobowamu anali pa ulendo kuchokera ku Yerusalemu, mneneri Ahiya wa ku Silo adampeza pa mseu. Ahiyayo anali atavala mwinjiro watsopano, ndipo aŵiriwo anali okha kuthengoko. Tsono Ahiya adagwira mwinjiro watsopano adaavalawo, nkuung'amba m'zidutswa khumi ndi ziŵiri. Ndipo adauza Yerobowamu kuti, “Iwe utengeko zidutswa khumi. Pakuti Chauta, Mulungu wa Aisraele, akunena kuti, ‘Ndithudi, Ine ndikuchotsa ufumu m'manja mwa Solomoni, ndipo iwe ndidzakupatsa mafuko khumi. Solomoni ndidzamsiyira fuko limodzi, chifukwa cha Davide mtumiki wanga, ndiponso chifukwa cha Yerusalemu, mzinda umene ndausankha pa mafuko onse a Aisraele. Ndidzachita zimenezi chifukwa Solomoniyo wandisiya Ine, wayamba kupembedza Asitoreti, mulungu wamkazi wa Asidoni, Kemosi mulungu wa Amowabu, ndi Milikomu mulungu wa Aamoni. Choncho sadandimvere, sadachite zimene ine ndifuna, ndipo sadasunge malamulo anga ndi malangizo anga, monga momwe ankachitira Davide, bambo wake. Komabe sindidzamlanda ufumu iyeyo. Adzakhalabe wolamulira masiku onse a moyo wake, chifukwa cha Davide mtumiki wanga amene ndidamsankha, amene ankasunga malamulo anga. Tsono ufumuwo ndidzauchotsera m'manja mwa mwana wake, ndipo iwe ndidzakupatsa mafuko khumi. Komabe mwana wake ndidzamsiyira fuko limodzi kuti pakhalebe Davide mtumiki wanga azidzakhala ndi nyale nthaŵi zonse pamaso panga ku Yerusalemu, mzinda umene ndausankha kuti azindipembedza kumeneko. Ndidzatenga iweyo Yerobowamu, udzalamulira paliponse pamene mtima wako ufuna, ndipo udzakhala mfumu ya Israele. Ukamamvera zonse zimene ndikukulamula, ndi kumayenda m'njira zanga, ndi kumachita zimene Ine ndifuna, posunga malamulo anga monga m'mene ankachitira Davide, mtumiki wanga, ndiye kuti Ine ndidzakhala nawe. Ndipo zidzukulu zako zidzalamulira monga m'mene ndidalonjezera Davide. Chigawo cha Israele ndidzachipereka kwa iwe. Chifukwa cha kuchimwa kwa Solomoniku, ndidzazunza zidzukulu za Davide, koma osati nthaŵi zonse ai.’ ” Nchifukwa chake Solomoni ankafunitsitsa kupha Yerobowamu. Koma Yerobowamu adachoka nathaŵira ku Ejipito, kwa Sisake mfumu yakumeneko. Adakhala kumeneko mpaka Solomoni atamwalira. Tsono ntchito zina za Solomoni, ndi zonse zimene adachita, ndiponso nzeru zake, zidalembedwa m'buku la Ntchito za Solomoni. Iye adalamulira Aisraele ku Yerusalemu zaka makumi anai. Tsono Solomoni adamwalira, naikidwa m'manda mu mzinda wa Davide, bambo wake. Ndipo Rehobowamu, mwana wake, adaloŵa ufumu m'malo mwake. Tsono Rehobowamu adapita ku Sekemu. Apo nkuti Aisraele onse atapita kale ku Sekemuko, kuti akamulonge ufumu. Nthaŵi imeneyo nkuti Yerobowamu, mwana wa Nebati, adakali ku Ejipito, momwe adaathaŵira mfumu Solomoni muja. Tsono atamva zaufumuzo, Yerobowamu adabwerera kuchokera ku Ejipitoko. Anthu adakamuitana. Choncho Yerobowamu pamodzi ndi anthu onse a ku Israele adadza kwa Rehobowamu namuuza kuti, “Bambo wanu ankatisenzetsa goli lolemetsa kwambiri. Ndiye ife tikuti inu tsopano mudzatipepukitsireko goli lolemetsayo ndi ntchito zoŵaŵazo zimene bambo wanu adatisenzetsa, apo ife tidzakutumikirani.” Rehobowamu adauza anthuwo kuti, “Pitani mukabwerenso kuno patapita masiku atatu.” Choncho anthuwo adachoka. Apo mfumu Rehobowamu adapempha nzeru kwa madoda amene ankakhala ndi bambo wake Solomoni ndi kumamlangiza akali moyo. Adaŵafunsa kuti, “Kodi mungandilangize zotani, kuti ndiŵayankhe anthu ameneŵa?” Madodawo adamuuza kuti, “Mukamatumikira bwino anthu ameneŵa nkukhaladi mtumiki wao, muzilankhula nawo mau abwino, ndipo iwowo adzakutumikirani mpaka muyaya.” Koma Rehobowamu adanyozera zimene madoda aja adaamlangiza, nakapempha nzeru kwa achinyamata anzake, amene adaakula naye pamodzi namamtumikira. Adaŵafunsa kuti, “Kodi mungandilangize zotani kuti tiŵayankhe anthu ameneŵa amene andipempha kuti ‘Tipeputsireniko goli limene bambo wanu adatisenzetsa?’ ” Anyamata anzakewo adamuuza kuti, “Anthuwo akupemphani kuti, ‘Bambo wanu adatisenzetsa goli lolemera, koma inu mutipeputsireko.’ Inu tsono mukaŵayankhe kuti, ‘Chala changa chakaninse nchachikulu kupambana chiwuno cha bambo wanga! Ndiye kuti bambo wanga ankakusenzetsani goli lolemetsa, kuyambira pano ine ndidzaonjezerapo. Bambo wanga ankakukwapulani ndi zikoti wamba, koma ine ndidzakukwapulani ndi mikwapulo yachitsulo.’ ” Tsono Yerobowamu pamodzi ndi anthu onse adabwera kwa Rehobowamu mkucha wake, monga momwe mfumu idaanenera kuti, “Mubwerenso kuno mkucha.” Ndiye mfumuyo idaŵayankha anthuwo mwankhanza. Idanyozera malangizo a madoda aja, nilankhula nawo anthuwo potsata malangizo a anyamata anzake, nkunena kuti, “Bambo wanga ankakusenzetsani goli lolemetsa, koma ine ndidzaonjezerapo. Bambo wanga ankakukwapulani ndi zikoti wamba, koma ine ndidzakukwapulani ndi mikwapulo yachitsulo.” Choncho mfumuyo sidamvere pempho la anthuwo, pakuti Chauta anali atazikonzeratu zinthuzo, kuti zichitikedi zimene adaalankhula ndi Yerobowamu, mwana wa Nebati, kudzera mwa Ahiya wa ku Silo. Tsono Aisraele onse akumpotowo ataona kuti mfumu sidamvere zimene ankapemphazo, adayankha mfumuyo kuti, “Kodi ife tili ndi gawo lanjinso m'banja la Davide? Sitingayembekeze choloŵa chilichonse m'banja la mwana wa Yese. Ndiye inu Aisraele, bwererani ku mahema kwanu! Tsopano iwe mwana wa Davide, udziwonere wekha pa banja lako.” Choncho Aisraelewo adachoka napita ku nyumba zao. Koma Rehobowamu adakhala akulamulirabe Aisraele enawo okhala m'mizinda ya Yuda. Tsono mfumu Rehobowamu adatuma Adoramu, amene ankayang'anira ntchito yathangata, koma Aisraele onse adamponya miyala mpaka kumupha. Pamenepo mfumu Rehobowamu adakwera msangamsanga pa galeta, nathaŵira ku Yerusalemu. Motero Aisraele akumpoto adakhala akupandukira banja la Davide mpaka lero lino. Tsono a ku Israele onse atamva kuti Yerobowamu wabwerera kuchokera ku Ejipito, adatumiza mau okamuitana kuti afike ku msonkhano. Kumeneko adamlonga ufumu wolamulira a ku Israele onse. Padaalibe wa ku Israele ndi mmodzi yemwe amene ankatsata ulamuliro wa banja la Davide, kupatula fuko la Yuda lokha. Tsono Rehobowamu atafika ku Yerusalemu, adasonkhanitsa ankhondo 180,000 a fuko la Yuda ndi la Benjamini ndi cholinga chakuti akamenyane ndi mafuko a ku Israele, kuti choncho amubwezere Rehobowamu ufumu wake. Koma Mulungu adadza kwa Semaya, mneneri wake, namlamula kuti, “Ukauze Rehobowamu, mwana wa Solomoni, mfumu ya ku Yuda, ndiponso anthu onse a fuko la Yuda ndi la Benjamini kuti, ‘Ine Chauta ndikuti musapite kukamenyana ndi abale anu a ku Israele. Aliyense abwerere kwao, poti zimene zachitikazi zachokera kwa Ine.’ ” Anthuwo adamvera mau a Chauta, nabwerera kwao monga momwe Chauta adaŵalamulira. Yerobowamu, mfumu yakumpoto, adamanganso mzinda wa Sekemu ku dziko la mapiri la Efuremu nakhala kumeneko. Kuchokera kumeneko adapita kukamanganso mzinda wa Penuwele. Yerobowamuyo ankaganiza mumtima mwake kuti, “Monga m'mene zilirimu, ufumu udzabwereranso ku banja la Davide. Anthu ameneŵa akamapita kukapereka nsembe ku Nyumba ya Chauta ku Yerusalemu, mitima yao idzabwerera kwa mbuyao Rehobowamu, mfumu ya ku Yuda, ndipo adzandipha.” Motero mfumuyo itaganizaganiza pa zimenezi, idapanga mafano aŵiri a anaang'ombe agolide. Tsono idauza anthu kuti, “Inu anthu a ku Israele, ku Yerusalemu mwakhala mukupitako nthaŵi yaitali. Tsopano milungu yanu ndi iyi imene idakutulutsani ku dziko la Ejipito.” Pamenepo Yerobowamu adatenga fano lina nkuliika ku Betele, lina nkuliika ku Dani. Ndipo zimenezi zidachimwitsa a ku Israele, poti anthuwo ena ankapita kukapembedza fano la ku Betele, ena ankakapembedza fano la ku Dani. Yerobowamu adamanganso nyumba pa malo achipembedzowo nasankha ansembe pakati pa anthu amene sanali Alevi. Ndipo Yerobowamu adakhazikitsa tsiku lachikondwerero, pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chitatu, lofanafana ndi tsiku lachikondwerero limene ankachita ku Yuda, napereka nsembe pa guwa nthaŵi imeneyo. Adachita zimenezi ku Betele, namapereka nsembe kwa mafano a anaang'ombe, amene iyeyo adapanga. Ndipo ku Beteleko adaikako ansembe pa malo achipembedzo amene adamanga. Yerobowamuyo ankapita ku guwa limene adamanga, pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chitatu, mwezi umene iye yekha adausankha. Motero Yerobowamu adalamula kuti pakhale tsiku lachikondwerero la Aisraele, ndipo iye yemwe adapita kukapereka nsembe yofukiza lubani pa guwa. Tsono mneneri wa Mulungu adachokera ku Yuda napita ku Betele monga momwe Chauta adaamlamulira. Nthaŵi imeneyo nkuti Yerobowamu ataimirira pambali pa guwa akufukiza lubani. Ndipo mneneriyo adatemberera guwalo potsata mau a Chauta nati, “Guwa iwe, guwa iwe, imva mau a Chauta, akunena kuti, ‘Mwana wamwamuna adzabadwa pa banja la Davide, dzina lake Yosiya. Pa iwe iyeyo adzaperekapo ngati nsembe ansembe otumikira ku malo achipembedzo amene amafukiza lubani pa iwe, ndipo pa iwe adzatenthapo mafupa a anthu.’ ” Tsono mneneri uja adapereka chizindikiro pa tsiku lomwelo nati, “Chizindikiro chimene Chauta wanena ndi ichi, ‘Guwali lidzang'ambika ndipo phulusa limene lili pamenepo lidzamwazika.’ ” Mfumu Yerobowamu atamva zimene ankanena mneneri wa Mulungu zija za guwa la ku Betele, adatambalitsa dzanja lake ali kuguwako nati, “Mgwireni.” Pomwepo dzanja lake lomwe adaatambalitsira mneneri wa Mulungu lija lidauma kuti gwa, ndipo sadathenso kulibweza. Nthaŵi yomweyo guwa lija nalonso lidang'ambika, ndipo phulusa lapaguwapo lidamwazika potsata chizindikiro chimene adaapereka mneneri wa Mulunguyo, malinga ndi m'mene adaanenera Chauta. Apo mfumu idauza mneneri wa Mulungu uja kuti, “Mupemphere kwa Chauta Mulungu wanu kuti andikomere mtima, dzanja langali lichire.” Mneneri wa Mulungu adapemphera kwa Chauta, ndipo dzanja la mfumu lidachiradi. Tsono mfumuyo idauza mneneri wa Mulungu uja kuti, “Tiyeni kunyumba mukadye chakudya, ndipo ndikakupatsani mphotho.” Koma mneneri wa Mulungu uja adauza mfumu kuti, “Ngakhale mundipatse theka la chuma chanu, sindikadya chakudya chilichonse kapena kumwa madzi kuno. Pakuti Chauta adandilamula kuti, ‘Usakadye chakudya chilichonse, kapena kumwa madzi, kapenanso kudzera njira yomwe udaadzera kale pobwera.’ ” Motero mneneriyo adadzera njira ina, osatsata njira imene adaadzera popita ku Betele. Tsono ku Betele kunkakhala mneneri wina wokalamba. Ana ake adadza kudzamuuza zonse zimene mneneri wa Mulungu adaachita ku Betele tsiku lija. Adauzanso atate ao mau onse amene mneneri wa Mulungu uja adaauza mfumu. Ndipo bambo wao uja adaŵafunsa kuti, “Kodi adadzera njira iti?” Ana akewo adamlangiza njira imene adadzera mneneri wa Mulungu wochokera ku Yuda uja. Bambo uja adauza ana akewo kuti, “Mangireni chishalo pa bulu.” Anawo adamanga chishalocho pa bulu, ndipo nkhalamba ija idakwerapo. Idalondola mneneri wa Mulungu uja, nikampeza atakhala pansi patsinde pa mtengo wa thundu. Tsono idamufunsa kuti, “Kodi inu ndiye mneneri wa Mulungu amene mudachoka ku Yuda?” Munthu uja adayankha kuti, “Ndine amene.” Nkhalambayo idati, “Tiyeni kwathu tikadye.” Koma mneneriyo adati, “Ine sindingabwerere nanu kapena kukaloŵa m'nyumba mwanu. Sindikadya chakudya kapena kumwa nanu madzi kuno. Pakuti Chauta adandiwuza kuti, ‘Usakadye chakudya kapena kumwa madzi kumeneko, kapenanso kubwerera podzera njira imene udaadzera popita.’ ” Nkhalambayo idamuuza kuti, “Inenso ndine mneneri monga inu nomwe, ndipo mngelo adalankhula nane nandiwuza kuti, ‘Ubwerere naye limodzi kunyumba kwako, kuti akadye chakudya ndiponso akamweko madzi.’ ” Nkhalambayo inkamuuza zabodza. Motero idabwerera naye limodzi kunyumba kwake, ndipo adakadya namwa madzi. Nthaŵi imene analikudya, Chauta adalankhula ndi mneneri wokalamba uja amene adaabweza mnzakeyo, ndipo iyeyo adafuulira mneneri wa Mulungu, wochokera ku Yuda uja kuti, “Imvani mau a Chauta, akuti chifukwa choti simudamvere mau a Chauta, ndipo simudatsate lamulo lake limene adakulamulani, koma mwabwerera, ndipo mwadya ndi kumwa madzi pa malo amene Chauta adakuuzani kuti musakadye chakudya kapena kumwako madzi, mtembo wanu sadzauika m'manda a makolo anu.” Choncho atatha kudya ndi kumwa, adamangirira chishalo pa bulu wa mneneri wa ku Yuda uja. Iyeyo popita, adakumana ndi mkango pa mseu, ndipo udamupha. Tsono mtembo udagwera mu mseu, ndipo bulu uja adaima pambali pa mtembowo. Mkango uja nawonso udaima pambali pa mtembowo. Anthu ena amene ankapita mumseumo, adaona mtembo uli gone, mkango utaima pambali pake. Ndipo adapita namakasimbira anzao mu mzinda za zimene adaaona pamseu paja. Mneneri amene adaabweza mnzake kunjira uja, atamva zimenezo, adati, “Ameneyo ndi mneneri wa Mulungu uja amene sadamvere mau a Chauta. Nchifukwa chake Chauta wampereka kwa mkango, umene wamkadzula ndi kumupha, monga momwe Chauta adaanenera.” Pompo mneneri wokalamba uja adauza ana ake kuti, “Mundimangire chishalo pa bulu.” Anawo adamangirira chishalocho. Tsono adapita, nakapeza mtembo wa munthu uja uli gone pa mseu, bulu ataima pambali pake pamodzi ndi mkango womwe. Mkangowo sudadye mtembowo kapena kukadzula bulu uja ai. Mneneri wokalambayo adatenga mtembo wa mneneri wa Mulungu uja, nauika pa buluyo, ndipo adabwera nawo ku mzinda kuti alire maliro ndi kuika mtembowo m'manda. Tsono adaika mtembowo m'manda ake. Pomulira ankati, “Mbale wanga ine! Mbale wanga ine!” Ndipo atamuika m'manda adauza ana ake kuti, “Ine ndikafa mudzandiike m'manda m'mene mneneri wa Mulunguyu waikidwa. Mudzaike mtembo wanga pambali pa mtembo wake. Zoonadi, zimene Chauta adalankhulitsa mneneriyo zotemberera guwa la ku Betele ndi nyumba za pa malo achipembedzo zimene zili m'mizinda ya ku Samariya, zidzachitikadi.” Ngakhale zidaatero, Yerobowamu sadasiye njira zake zoipa, koma adaikanso anthu wamba kukhala ansembe pa malo akeake achipembedzo. Aliyense amene ankafuna, adampatula kuti akhale wansembe wa pa malowo. Limeneli linali tchimo lalikulu pa banja la Yerobowamu. Nchifukwa chake banjalo lidaonongeka ndi kufafanizika pa dziko lapansi. Pa nthaŵi imeneyo Abiya, mwana wa Yerobowamu, adayamba kudwala. Ndiye Yerobowamu adauza mkazi wake kuti, “Tiye udzizimbaitse, munthu asakudziŵe kuti ndiwe mkazi wa Yerobowamu, ndipo upite ku Silo kwa mneneri Ahiya, amene adanena za ine, kuti ndidzakhala mfumu yolamulira anthu aŵa. Utenge mitanda khumi yabuledi, makeke ndiponso botolo la uchi, upite kwa iyeyo. Iye adzakuuza zimene zidzamuwonekere mwanayu.” Mkazi wa Yerobowamu adadzizimbaitsadi, ndipo adapita ku Silo, nakafika ku nyumba ya Ahiya. Ahiya sankatha kupenya bwino, ankangoona ngati nkhungu, chifukwa cha ukalamba. Chauta adauza Ahiya kuti, “Taona, mkazi wa Yerobowamu akubwera kudzafunsa iwe za mwana wake, pakuti akudwala. Ndiye iwe udzamuuze zakutizakuti mkaziyo. Akafika adzadzibisa, nkukhala ngati mkazi wina.” Tsono Ahiya atangomva mgugu wa mapazi ake akuloŵa pa khomo, adati “Loŵa, iwe mkazi wa Yerobowamu, bwanji ukudzibisa? Ndakutengera mau oŵaŵa. Pita, kamuuze Yerobowamu kuti Chauta, Mulungu wa Israele, akuti, ‘Ine ndidakukweza pakati pa anthu, ndipo ndidakusandutsa mtsogoleri wa anthu anga a ku Israele. Ndidachotsa ufumu ku banja la Davide ndi kuupereka kwa iwe. Komabe iwe sudafanefane ndi Davide mtumiki wanga, amene ankamvera malamulo anga, ndipo ankanditsata ndi mtima wake wonse, namachita zimene Ine ndimafuna. Koma iwe wachita zoipa kupambana onse amene analipo kale, iwe usanakhale pa mpando waufumu, pakuti wadzipangira milungu ina ndiponso mafano osungunula. Pakutero wandipsetsa mtima kwabasi. Ineyo wanditayiratu kumbuyo. Nchifukwa chake ndidzagwetsa mavuto pa banja lako, iwe Yerobowamu. Ndidzaononga mwamuna aliyense wa pa banja lako, kapolo pamodzi ndi mfulu yomwe, m'dziko la Israele. Ndidzaononga kwathunthu banja la Yerobowamu monga m'mene munthu amachotsera ndoŵe pa bwalo mpaka yonse itatha. Aliyense m'banja la Yerobowamu, amene adzafere mu mzinda, agalu adzamudya. Aliyense amene adzafere ku thengo, mbalame zidzamudya. Ndatero Ine Chauta.’ Nchifukwa chake tsono nyamuka, upite kunyumba kwako. Phazi lako likangoponda mumzindamo, mwanayo adzafa. Aisraele onse adzalira maliro ake, ndipo adzamuika, pakuti iye yekhayo mwa anthu a m'banja la Yerobowamu ndiye adzaikidwe ku manda, chifukwa Chauta, Mulungu wa Aisraele, wakondwa ndi iye yekha pa banja lonse la Yerobowamu. Kuwonjezera pamenepo, Chauta adzadzisankhira mfumu yolamulira a ku Israele, imene idzaonongeretu banja la Yerobowamu. Tsiku lake ndi lero, wamvatu! Chauta adzagwedeza Israele ngati bango lapamadzi, ndipo adzachotsa anthu a ku Israele m'dziko labwinoli, limene Iye adapatsa makolo ao. Adzaŵamwazira kutsidya kwa mtsinje wa Yufurate, chifukwa choti iwo adadzipangira mafano a Asera, mulungu wachikazi, nakwiyitsa Chauta pakutero. Choncho Chauta adzaŵataya a ku Israele chifukwa cha zoipa za Yerobowamu, zimene adachita iye mwini ndi kuŵachimwitsanso Aisraelewo.” Tsono mkazi wa Yerobowamu adachoka napita ku Tiriza. Atangofika pa khomo la nyumba yake, mwana uja adamwalira. Aisraele adamuika, nalira maliro ake, monga momwe Chauta adaanenera kudzera mwa mneneri Ahiya. Tsono ntchito zonse za Yerobowamu, m'mene ankamenyera nkhondo ndi m'mene ankalamulira, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a Aisraele. Nthaŵi imene Yerobowamu adakhala mfumu idakwana zaka makumi aŵiri. Ndipo adamwalira, naikidwa m'manda. Pambuyo pake Nadabu mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Rehobowamu, mwana wa Solomoni, anali mfumu ya ku Yuda. Anali wa zaka 41 nthaŵi imene ankaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 17 ku Yerusalemu, mzinda umene Chauta adaausankha pakati pa mafuko onse a Aisraele, kuti anthu azimpembedzerako. Mai wake anali Naama, wa kwa Aamoni. Masiku amenewo anthu a ku Yuda ankachita zoipa, ankachimwira Chauta kupambana m'mene adaachitira makolo ao onse, nakwiyitsa Mulungu. Pakuti iwonso adadzimangira akachisi opembedzerapo mafano pa zitunda zina, ndi kuimika miyala ndi mitengo yachipembedzo pa phiri lalitali lililonse, ndiponso patsinde pa mtengo uliwonse wogudira. Kuwonjezera pamenepo, m'dzikomo munkapezeka anthu ena ochitana zadama potsata chipembedzo chao. Anthu ankachita zonyansa zonse zimene inkachita mitundu ya anthu amene Chauta adaaipirikitsa pofika Aisraele. Chaka chachisanu cha ufumu wa Rehobowamu, Sisake, mfumu ya ku Ejipito, adabwera kudzathira Yerusalemu nkhondo. Adalanda chuma cha ku Nyumba ya Chauta pamodzi ndi chuma cha ku nyumba ya mfumu. Adatenga zonse, ngakhalenso zishango zomwe zagolide zimene Solomoni adaapanga. Pambuyo pake mfumu Rehobowamu adapanga zishango zamkuŵa m'malo mwake, nazipereka m'manja mwa akapitao a alonda amene ankalonda pakhomo pa nyumba ya mfumu. Tsono nthaŵi zonse mfumu ikamaloŵa m'Nyumba ya Chauta, alondawo ankatenga zishangozo, kenaka nkumazibwezera ku chipinda cha alonda. Tsono ntchito zina za Mfumu Rehobowamu, ndi zonse zimene adazichita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda. Panali nkhondo zosalekeza pakati pa Rehobowamu ndi Yerobowamu. Ndipo Rehobowamu adamwalira, naikidwa mu mzinda wa Davide m'manda momwe adaikidwa makolo ake. Mai wake uja anali Naama, wa mtundu wa Aamoni. Ndipo Abiya, mwana wa Rehobowamu, adaloŵa ufumu m'malo mwa bambo wake. Pa chaka cha 18 cha ufumu wa Yerobowamu mwana wa Nebati, Abiya adaloŵa ufumu wa ku Yuda. Adakhala mfumu mu Yerusalemu zaka zitatu. Mai wake anali Maaka, mwana wa Abisalomu. Ndipo Abiyayo adatsatira zoipa zonse zimene ankachita bambo wake. Sadatsate Chauta moona monga Davide kholo lake. Komabe chifukwa cha Davideyo, Chauta adapatsa Abiya mwana, kuti azilamulira ku Yerusalemu, iyeyo atafa. Zidatero chifukwa choti Davide adaachita zolungama pamaso pa Chauta, poti sadapatuke pa zimene Chauta adamlamula masiku onse a moyo wake, kupatula nkhani yokha ija ya Uriya Muhiti uja. Panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobowamu masiku onse a moyo wa Abiyayo. Tsono ntchito zina za Abiya ndi zonse zimene adazichita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda. Tsono Abiya adamwalira, naikidwa m'manda momwe adaikidwa makolo akewo mu mzinda wa Davide. Ndipo Asa mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Pa chaka cha 20 cha ufumu wa Yerobowamu mfumu ya ku Israele, Asa adaloŵa ufumu wa ku Yuda, ndipo adalamulira zaka 41 ku Yerusalemu. Gogo wake wamkazi anali Maaka, mwana wa Abisalomu. Asa adachita zolungama pamaso pa Chauta monga m'mene adachitira Davide kholo lake. Adachotsa anthu onse m'dzikomo amene ankachitana zadama potsata chipembedzo chao, nachotsanso mafano onse amene makolo ake adaapanga. Adachotsanso gogo wake Maaka pa udindo wa mfumukazi, chifukwa choti ankapembedza fano lonyansa la Asera. Ndipo Asa adaliphwanya fanolo, nakalitenthera ku khwaŵa la Kidroni. Akachisi okha opembedzerapo mafano sadaŵaononge. Komabe mtima wa Asa udakhala wokhulupirika kwa Chauta masiku onse a moyo wake. Tsono Asayo adabwera nazo ku Nyumba ya Chauta zopereka za bambo wake ndiponso zopereka zakezake za siliva, golide ndi ziŵiya. Panali nkhondo pakati pa Asa ndi Baasa, mfumu ya ku Israele, nthaŵi yonse ya ufumu wao. Baasayo adapita kukathira nkhondo dziko la Yuda, namangira linga mzinda wa Rama, kuti aziletsa anthu kuloŵa kapena kutuluka m'dziko la Asa, mfumu ya ku Yuda. Tsono Asa adatenga siliva yense pamodzi ndi golide, zimene zinatsala ku malo osungira chuma cha ku Nyumba ya Chauta ndiponso ku nyumba ya mfumu, napatsira atumiki ake. Ndipo adaŵatuma kuti akazipereke Benihadadi, mwana wa Tabirimoni mdzukulu wa Heziyoni, mfumu ya ku Siriya, amene ankakhala ku Damasiko. Mau a Asa anali akuti, “Tiye tigwirizane ine ndi iwe, monga m'mene ankachitira bambo wanga ndi bambo wako. Ona, ndikukutumizira mphatso za siliva ndi golide. Pita ukaphwanye chigwirizano chako ndi Baasa, mfumu ya ku Israele, kuti sadzandithiranso nkhondo.” Benihadadi adamvera zimene adanena mfumu Asa zija, motero adatuma atsogoleri a magulu ake ankhondo kukathira nkhondo mizinda ya ku Israele. Adagonjetsa Iyoni, Dani, Abele-Beti-Maaka ndi dera lonse Kineroti pamodzi ndi dziko lonse la Nafutali lomwe. Tsono Baasa atazimva zimenezi, adaleka kumangira Rama linga, nakakhala ku Tiriza. Apo mfumu Asa adaitana anthu onse a ku Yuda, osasiya ndi m'modzi yemwe, kuti adzanyamule miyala ndi mitengo, imene Baasa ankamangira linga la Rama. Zimenezi mfumu Asa adamangira linga la Geba m'dziko la Benjamini, ndiponso la Mizipa. Tsono ntchito zina za Asa, zamphamvu zake zonse, zinthu zimene adazichita ndi mizinda imene adaimanga, zonsezo zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda. Koma pa nthaŵi ya ukalamba wake adadwala nthenda ya miyendo. Ndipo adamwalira, naikidwa m'manda momwe adaikidwa makolo akewo mu mzinda wa Davide kholo lake. Mwana wake Yehosafati ndiye adaloŵa ufumu m'malo mwake. Nadabu, mwana wa Yerobowamu, adayamba kulamulira anthu a ku Israele pa chaka chachiŵiri cha ufumu wa Asa wa ku Yuda. Tsono Nadabuyo adalamulira ku Israele zaka ziŵiri. Iyeyo adachita zoipa pamaso pa Chauta, nayenda njira za bambo wake, ndipo zoipa zakezo adachimwitsa nazo anthu a ku Israele. Tsono Baasa mwana wa Ahiya, wa banja la Isakara, adachita chiwembu Nadabuyo. Adamupha ku Gibetoni, mzinda wa Afilisti, pamene Nadabu ndi anthu a ku Israele ankathira nkhondo mzindawo. Baasa adapha Nadabu pa chaka chachitatu cha ufumu wa Asa wa ku Yuda, naloŵa ufumu m'malo mwake. Atangoloŵa ufumuwo, adapha anthu onse a banja la Yerobowamu. Sadasiyepo ndi mmodzi yemwe wamoyo pa banjapo, mpaka adaonongeratu banja lonselo, malinga ndi mau amene Chauta adaalankhula kudzera mwa mtumiki wake uja Ahiya wa ku Silo. Zimenezi zidachitika chifukwa cha machimo a Yerobowamu ndi zimene adachimwitsa nazo anthu a ku Israele, naputa nazo mkwiyo wa Chauta, Mulungu wa Aisraele. Tsono ntchito zina za Nadabu, ndi zonse zimene adazichita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele. Ndipo panali nkhondo pakati pa Asa ndi Baasa masiku onse a ufumu wao. Chaka chachitatu cha ufumu wa Asa wa ku Yuda, Baasa mwana wa Ahiya adayamba kulamulira anthu a ku Israele ku Tiriza, ndipo adakhala mu ufumu zaka 24. Iyeyo adachita zoipa pamaso pa Chauta ndipo ankayenda m'njira zoipa za Yerobowamu, namachita zimene adachimwitsa nazo anthu a ku Israele. Chauta adalankhula kudzera mwa mneneri Yehu, mwana wa Hanani, mau odzudzula Baasa akuti, “Iwe sudaali kanthu konse, ndidachita kukukweza kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga a ku Israele. Komabe tsopano wachimwa ngati Yerobowamu, ndipo waŵachimwitsa anthu a ku Israelewo, mwakuti iwo aputa mkwiyo wanga chifukwa cha kuchimwa kwaoko. Ndithudi ndidzakufafaniza kotheratu pamodzi ndi banja lako lonse, monga m'mene ndidachitira banja la Yerobowamu mwana wa Nebati. Aliyense wa banja la Baasa amene adzafere mu mzinda, agalu adzamudya. Ndipo aliyense amene adzafere ku thengo, mbalame zamumlengalenga zidzamudya.” Ntchito zina za Baasa ndi zonse zamphamvu zimene adachita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele. Baasa adamwalira, naikidwa m'manda ku Tiriza. Ndipo Ela mwana wake ndiye adaloŵa ufumu m'malo mwake. Asanafe Baasa, Chauta adalankhula kudzera mwa mneneri Yehu, mwana wa Hanani, mau omuzenga mlandu Baasa pamodzi ndi banja lake lonse, chifukwa cha zoipa zonse zimene adaachita pamaso pa Chauta. Iyeyo adaputa mkwiyo wa Chauta ndi machimo amene ankachita, olingana ndi a anthu a banja la Yerobowamu, ndiponso chifukwa choti adaaonongeratu banja lonse la Yerobowamu. Chaka cha 26 cha ufumu wa Asa wa ku Yuda, Ela mwana wa Baasa adaloŵa ufumu wa ku Israele ku Tiriza, ndipo adalamulira zaka ziŵiri. Tsono munthu wina dzina lake Zimuri, amene anali mkulu woyang'anira hafu la magaleta ake, adamchita chiwembu. Pamene Elayo anali ku Tiriza, namamwa mpaka kuledzera m'nyumba ya Ariza, amene ankayang'anira nyumba yachifumu ku Tirizako, Zimuri adadzaloŵa, napha Elayo. Chinali chaka cha 27 cha ufumu wa Asa wa ku Yuda. Tsono Zimuriyo adaloŵa ufumu m'malo mwa Ela. Zimuri atangoyamba kulamulira, adapha anthu onse a banja la Baasa. Sadamsiyirepo ndi mwamuna mmodzi yemwe mwa apachibale ake kapena abwenzi ake. Motero Zimuri adaononga banja lonse la Baasa monga momwe Chauta adaalankhulira kudzera mwa Yehu mneneri uja. Paja Yehuyo adaadzudzula Baasa chifukwa cha zoipa zake ndi za Ela mwana wake, zimene onse aŵiriwo adaachita. Iwo adachimwitsa anthu a ku Israele, naputa mkwiyo wa Chauta, Mulungu wa Aisraele, chifukwa cha mafano ao. Tsono ntchito zina za Ela ndi zonse zimene adazichita zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele. Chaka cha 27 cha ufumu wa Asa wa ku Yuda, Zimuri adaloŵa ufumu wa ku Israele ku Tiriza, koma adangolamulira masiku asanu ndi aŵiri okha. Nthaŵi imeneyo magulu ankhondo a Aisraele adaali akuzinga mzinda wa Gibetoni. Mzindawo unali wa Afilisti. Koma pamene ankhondowo adamva kuti Zimuri wachita chiwembu ndipo wapha mfumu, tsiku lomwelo kuzithando komweko onse adasankha Omuri mtsogoleri wankhondo kuti akhale mfumu ya Aisraele. Motero Omuri adachoka ku Gibetoni pamodzi ndi ankhondo ake onse, nakazinga mzinda wa Tiriza. Zimuri ataona kuti mzinda walandidwa, adathaŵira ku nsanja yam'kati ya nyumba ya mfumu. Adatentha nyumbayo, iye nafera momwemo. Adafa choncho chifukwa cha zoipa zake zimene adachita pamaso pa Chauta. Iyeyo ankayenda m'njira zoipa za Yerobowamu, nachimwitsa nazo Aisraele. Tsono ntchito zina zonse za Zimuri, ndi chiwembu chimene adachita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele. Tsono Israele adagaŵikanso pakati, ena adatsata Tibini mwana wa Ginati, kuti amlonge ufumu, ndipo ena adatsata Omuri. Koma anthu otsata Omuri adagonjetsa anthu otsata Tibini, mwana wa Ginati. Choncho Tibini adafa, ndipo Omuri adaloŵa ufumu. Chaka cha 31 cha ufumu wa Asa wa ku Yuda, Omuri adaloŵa ufumu wa dziko la Israele, ndipo adalamulira zaka khumi ndi ziŵiri. Ku Tiriza adalamulirako zaka zisanu ndi chimodzi. Iyeyo adagula phiri la Samariya kwa Semeri pa mtengo wa ndalama 6,000 zasiliva. Ndipo adamangapo mzinda, namanganso linga kutchinjiriza phirilo. Mzinda umene adaumangawo adautcha Samariya, potsata dzina la Semeri, mwini wake wa phirilo. Koma Omuri adachita zoipa pamaso pa Chauta ndipo zoipa zakezo zidaposa za mafumu ena onse akale. Ankachita zoipa ngati Yerobowamu, mwana wa Nebati, zimene adachimwitsa nazo anthu a ku Israele, naputa mkwiyo wa Chauta, Mulungu wa Aisraele, popembedza mafano. Ntchito zina zonse za Omuri zimene ankachita, ndi mphamvu zimene adaonetsa, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele. Ndipo Omuri adamwalira, naikidwa m'manda ku Samariya. Tsono Ahabu mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Chaka cha 38 cha ufumu wa Asa wa ku Yuda, Ahabu mwana wa Omuri, adaloŵa ufumu wa ku Israele. Iyeyo adalamulira anthu a ku Israele ku Samariya zaka 22. Koma Ahabu adachita zoipa pamaso pa Chauta kupambana mafumu onse akale. Adachita ngati sadakhutire ndi kuchimwa konga kwa Yerobowamu, mwakuti adaonjeza tchimo pakukwatira Yezebele, mwana wa Etibaala mfumu ya Asidoni, nayamba kutumikira fano lotchedwa Baala, ndi kumalipembedza. Adamanga nyumba ku Samariya yopembedzeramo Baala, ndipo m'nyumbamo adamangamo guwa la Baalayo, naimikamo fano la Asera. Motero Ahabu adachita zinthu zambiri zoputa mkwiyo wa Chauta, Mulungu wa Aisraele, kupambana mafumu onse a ku Israele amene adaalipo kale. Pa masiku a mfumu Ahabu, Hiyele wa ku Betele adamanganso mzinda wa Yeriko. Koma monga adaaneneratu Chauta kudzera mwa Yoswa mwana wa Nuni, Abiramu, mwana wamwamuna wachisamba wa Hiyele, adamwalira pa nthaŵi yomanga maziko a mzindawo. Kenaka Segubu, mzime wake, nayenso adamwalira pa nthaŵi yomanga zipata za mzindawo. Mneneri Eliya wa ku Tisibe ku Giliyadi, adauza Ahabu kuti, “Pali Chauta, Mulungu wa Aisraele, amene ndimamtumikira, sipakhala mame kapena mvula zaka zikubwerazi, mpaka ine ntanena.” Kenaka Chauta adauza Eliyayo kuti, “Chokako kuno, upite chakuvuma, ukabisale ku mtsinje wa Keriti, kuvuma kwa Yordani. Uzikamwa mumtsinjemo, ndipo ndalamula makwangwala kuti azikakudyetsa kumeneko.” Choncho Eliyayo adapita nakachita monga momwe Chauta adaanenera. Adapita nakakhala m'mbali mwa mtsinje wa Keriti kuvuma kwa Yordani. Tsono makwangwala ankadzampatsa buledi ndi nyama m'maŵa ndi madzulo. Ndipo ankamwa madzi kumtsinjeko. Patangopita kanthaŵi, mtsinjewo udaphwa, poti kunalibe mvula m'dzikomo. Tsono Chauta adauzanso Eliya kuti, “Nyamuka upite ku Zarefati, mudzi wa ku Sidoni, ndipo ukakhale kumeneko. Ndalamula mai wamasiye wakumeneko kuti azikakudyetsa.” Choncho Eliya adanyamuka napita ku Zarefati. Atafika pa chipata cha mzindawo, adangoona mai wamasiye akutola nkhuni. Tsono adaitana maiyo namuuza kuti, “Patseniko madzi pang'ono, ndimwe.” Pamene mai uja ankapita kukatunga madziwo, Eliya adamuitananso namuuza kuti, “Munditengerekonso kabuledi.” Apo maiyo adati, “Pali Chauta, Mulungu wanu, ine sindidaphike kanthu kalikonse, koma ndili ndi ufa pang'ono m'mbiya, ndi mafuta pang'ono m'nsupa. Tsono ndikutola nkhuni zoti ndikaphikire kaufako, kuti ndikadye ine ndi mwana wanga, kenaka kufa kukhala komweko.” Koma Eliya adauza maiyo kuti, “Musade nkhaŵa. Pitani, mukachite monga mwaneneramo. Koma poyamba mutapeko kaufa pang'ono, mundiphikire kakeke, mubwere nako kuno. Pambuyo pake mukaphikenso kuti mudye inuyo ndi mwana wanu. Chauta, Mulungu wa Aisraele, akunena kuti, ‘Ufa umene uli m'mbiyawo sudzatha, mafutanso amene ali m'nsupawo sadzatha, mpaka tsiku limene Chauta adzagwetse mvula pa dziko lapansi.’ ” Tsono maiyo adapita, nakachitadi monga momwe adaanenera Eliya. Maiyo ndi Eliya ndiponso onse a pa banja la maiyo adadya ufawo masiku ambiri. Ufa umene unali m'mbiyamo sudathe, mafuta amene anali m'nsupawo sadathenso, monga momwe Chauta adaalankhulira kudzera mwa Eliya. Tsiku lina mwana wa mkazi wamasiye uja, mwini wake nyumba, adadwala. Matenda adakula kwambiri, kotero kuti mwanayo adamwalira. Mkazi uja adafunsa Eliya kuti, “Kodi ndakulakwirani chiyani, inu mneneri wa Mulungu? Kodi mwadza kwa ine kuno kudzakumbutsa Mulungu machimo anga ndi kundiphera mwana wanga?” Eliya adauza maiyo kuti, “Tandipatsani mwanayo.” Pompo Eliya adatenga mwanayo pa mfukato ya mai uja, napita naye ku chipinda chapamwamba, kumene ankagona, ndipo adakamgoneka pa bedi lake. Kenaka Eliya adatama Chauta mopemba kuti, “Inu Chauta, Mulungu wanga, kodi mai wamasiyeyu, amene akundisunga, mwamchitiranji choipa chotere, pomuphera mwana wake?” Tsono adafungatira mwanayo katatu, natamanso Chauta mopemba kuti, “Inu Chauta, Mulungu wanga, mubwezereni moyo wake mwanayu.” Ndipo Chauta adamumvera Eliyayo. Pomwepo moyo wa mwana uja udabwereranso mwa iye natsitsimuka. Eliya adatenga mwanayo, natsika naye kuchoka m'chipinda chapamwamba chija, ndipo adampereka kwa mai wake. Tsono adauza maiyo kuti, “Onani, mwana wanu ali moyo.” Ndipo mai uja adauza Eliya kuti, “Tsopano ndikudziŵa kuti ndinu munthu wa Mulungu, ndipo Chauta walankhula kudzera mwa inu.” Patapita nthaŵi yaitali, pa chaka chachitatu cha chilala, Chauta adauza Eliya kuti, “Pita ukadziwonetse kwa Ahabu. Ndidzagwetsa mvula pa dziko lapansi.” Motero Eliya adapita kukadziwonetsa kwa Ahabu. Pamenepo nkuti njala itafika pake penipeni ku Samariya. Mfumu Ahabu adaitana Obadiya, amene ankayang'anira zonse za ku nyumba yachifumu. (Ndiye kuti Obadiya ankatumikira Chauta. Ndipo pamene Yezebele ankapha aneneri a Chauta, Obadiya adaabisa aneneri 100. Aneneri 50 adaŵabisa m'phanga lina, 50 ena m'phanga linanso, namaŵapatsa chakudya ndi madzi.) Tsono Ahabu adauza Obadiya kuti, “Tiye tiyendere dziko lonse, tiwone akasupe onse a madzi, ndiponso tipite ku zigwa zonse. Mwina mwake tingapeze udzu womadyetsa akavalo ndi abulu kuti akhale moyo.” Choncho Ahabu ndi Obadiya adagaŵana dzikolo kuti aliyendere. Ahabu adapita mbali ina, Obadiya mbali inanso. Pamene Obadiya ankapita pa ulendo wake, adangoona mneneri Eliya akubwera kudzakumana naye. Obadiya adamzindikira Eliyayo, ndipo adamuŵeramira, namufunsa kuti, “Kodi ndinudi mbuyanga Eliya?” Eliya adayankha kuti, “Ndine amene. Pita ukauze mbuyako kuti Eliya wabwera.” Obadiya adamufunsa kuti, “Kodi ndachimwa chiyani kuti inu mundipereke ine mtumiki wanu m'manja mwa Ahabu kuti andiphe? Pali Chauta, Mulungu wanu wamoyo, kulibe mtundu wa anthu kapena ufumu uliwonse kumene mbuyanga Ahabu sadatumeko anthu okakufunafunani. Anthu akamuuza kuti, ‘Eliya kulibe kuno,’ Ahabu ankaŵalumbiritsa anthuwo kuti atsimikizedi ngati inu kunalibe kumeneko. Ndiye ine mukuti ndipite ndikamuuze mbuyanga kuti mwabwera? Mwina ine ndikangochoka pano, pompo mzimu wa Chauta ukuchotsani kuno kunka nanu komwe ine sindidziŵa. Tsono ndikakamuuza Ahabu, iye osadzakupezani, adzandipha, ngakhale kuti mtumiki wanune ndakhala ndikutumikira Chauta kuyambira ubwana wanga. Kodi inu mbuyanga simudamve zoti nthaŵi imene Yezebele ankapha aneneri a Chauta, ine ndidabisa aneneri 100 a Chauta, anthu 50 m'phanga limodzi, 50 ena m'phanga lina, ndipo kuti ndinkaŵadyetsa chakudya ndi kumaŵapatsa madzi akumwa? Ndiye inu mukuti, ‘Pita, kamuuze mbuyako kuti, “Eliya wabwera?” ’ Ndithu iyeyo adzandipha ine!” Koma Eliya adati, “Ndithudi, pali Chauta Wamphamvuzonse amene ndimamtumikira, ine lero ndikukaonekera pamaso pa Ahabu.” Motero Obadiya adapita kwa Ahabu kukamuuza za Eliyayo. Ndipo Ahabu adapita kukakumana ndi Eliya. Tsono Ahabu ataona Eliya, adamuuza kuti, “Ha, iwe munthu wovuta anthu a ku Israele, wabweradi?” Eliya adayankha kuti, “Ameneyo sindine ai. Koma inuyo pamodzi ndi banja la bambo wanu, ndiye mwakhala mukuvuta anthu a ku Israele, chifukwa mwasiya malamulo a Chauta nkumatsata Abaala. Nchifukwa chake tsopano tumizani mau kuti musonkhanitse onse a ku Israele, kuti abwere, ndikakumane nawo ku Phiri la Karimele. Abwere ndi aneneri a Baala 450, ndiponso aneneri a fano la Asera 400, amene amadya kwa Yezebele.” Pamenepo Ahabu adatumiza mau kwa onse a ku Israele, ndipo adasonkhanitsa aneneri a Baala ku Phiri la Karimele. Eliya adasendera pafupi ndi anthu onsewo, naŵafunsa kuti, “Kodi mudzakhala anthu a mitima iŵiri mpaka liti? Ngati Chauta ndiye Mulungu, mtsateni. Koma ngati Baala ndiye Mulungu, tsatani iyeyo.” Anthuwo sadamuyankhe ndi liwu limodzi lomwe. Tsono Eliya adauza anthu aja kuti, “Ine ndatsala ndekha mwa aneneri a Chauta, koma aneneri a Baala alipo 450 pamodzi. Bwerani ndi ng'ombe zamphongo ziŵiri. Iwo asankhepo okha ng'ombe imodzi ndipo aidule nthulinthuli ndi kuziika pa nkhuni nthulizo, koma asasonkhepo moto ai. Inenso ndidula ng'ombe inayo nthulinthuli, ndi kuikanso nthulizo pa nkhuni, koma osasonkhapo moto ai. Inu mutame dzina la mulungu wanu mopemba, inenso nditana dzina la Chauta mopemba. Tsono Mulungu amene ayankhe potumiza moto, ameneyo ndiyedi Mulungu.” Pamenepo anthu onsewo adati, “Ai, mwanena bwino.” Tsono Eliya adauza aneneri a Baala aja kuti, “Yambani ndinu. Sankhulani ng'ombe yamphongo imodzi, muikonze, poti mwachuluka. Tsono mutame dzina la mulungu wanu mopemba, koma musasonkhe moto ai.” Iwowo adatenga ng'ombe yamphongo imene adaŵapatsa, naipha. Tsono adatama dzina la Baala mopemba, kuyambira m'maŵa mpaka masana, ponena kuti, “Inu a Baala, tiyankheni ife.” Aneneri a Baala aja ankalumphalumpha movina, kuzungulira guwa limene adaamangalo, koma sipadamveke ndi liwu lomwe, panalibe woyankha. Tsono nthaŵi yamasana ndithu Eliya adayamba kuŵaseka, naŵauza kuti, “Fuulani kwambiri, suja mukuti iyeyo ndi mulungu! Mwina mwaketu watanganidwa, kapena wapita kwina kukadzithandiza, kapena ali pa ulendo, kaya kapena ali m'tulo, ndiye kamdzutsenitu.” Aneneri a Baalawo ankafuula kwambiri, nadzichekacheka ndi malupanga ndi mipeni potsata miyambo yao, mpaka magazi chuchuchu m'mabalawo. Dzuŵa litapendeka, adakhala akufuulabe mopenga kufikira nthaŵi yoperekera nsembe idakwana. Komabe kunali zii! Osamveka ndi liwu lomwe. Panalibe woyankha, panalibe ndi mmodzi yemwe wosamalako zimenezo. Pamenepo Eliya adauza anthu onse aja kuti, “Senderani pafupi ndi ine.” Anthu onsewo adasenderadi kwa iyeyo. Tsono Eliya adakonza guwa la Chauta limene linali litagwetsedwa. Adatenga miyala khumi ndi iŵiri potsata chiŵerengero cha mafuko a ana a Yakobe amene Chauta adaamuuza kuti dzina lake lidzakhala Israele. Ndi miyalayo adamangira guwa lotamandirapo Chauta. Tsono adakumba ngalande kuzungulira guwalo. Kukula kwa ngalandeyo kunali ngati moloŵa mitsuko inai ya madzi. Adaika nkhuni zija m'malo mwake, nadula ng'ombe ija nthulinthuli, nkuika nthulizo pankhunipo. Pambuyo pake adauza anthu kuti, “Dzazani mitsuko inai ndi madzi, muŵathire pa nyama yansembeyo, ndi pa nkhunizo.” Ndipo adaŵauza kuti, “Bwerezaninso kachiŵiri.” Anthu aja adathiranso madziwo kachiŵiri. Adaŵauzanso kuti, “Thiraninso kachitatu,” nateronso kachitatu. Madziwo adayenderera kuzungulira guwalo, nadzaza ngalande yonse. Itakwana nthaŵi yake yopereka nsembe, mneneri Eliya adasendera pafupi ndi guwa nati, “Inu Chauta, Mulungu wa Abrahamu, Isaki ndi Israele, lero zidziŵike kuti Inuyo ndiye Mulungu m'dziko la Israele, ndipo kuti ine ndine mtumiki wanu, ndiponso kuti ndachita zonsezi chifukwa mwanena ndinu. Mundiyankhe, Inu Chauta, mundiyankhe, kuti anthu aŵa adziŵe kuti Inu Chauta ndinu Mulungu, ndipo kuti atembenuke mtima.” Pomwepo moto wa Chauta udagwa, nunyeketsa nsembe yopserezayo, nkhunizo, miyala ija ndi dothi lomwe. Motowo udaphwetsa ndi madzi omwe amene anali m'ngalande aja. Tsono anthu onse ataona zimenezo, adadzigwetsa pansi nanena mokweza kuti, “Chauta ndiyedi Mulungu! Chauta ndiyedi Mulungu!” Pamenepo Eliya adaŵauza kuti, “Gwirani aneneri onse a Baala. Asapulumukepo ndi mmodzi yemwe.” Motero adaŵagwira onsewo. Ndipo Eliya adatsikira nawo ku mtsinje wa Kisoni, nakaŵaphera kumeneko. Pambuyo pake Eliya adauza Ahabu kuti, “Pitani mukadye ndi kumwa, pakuti kukumveka mkokomo wa mvula.” Motero Ahabu adapita kukachita madyerero. Koma Eliya adakwera pamwamba pa Phiri la Karimele, ndipo adazyolikira pansi naika mutu wake pakati pa maondo ake. Tsono adauza mtumiki wake kuti, “Pita ukayang'ane ku nyanja.” Mtumikiyo adapita kukayang'ana, nati, “Kulibe kanthu.” Eliya adamuuza kuti, “Pitanso kasanunkaŵiri.” Mtumikiyo atapita kachisanu ndi chiŵiri adati, “Pali kamtambo kakang'ono konga dzanja la munthu, kakutuluka kunyanjako.” Pompo Eliya adati, “Pita kamuuze Ahabu kuti akonze galeta lake, ndipo azipita, kuti mvula ingamtsekereze.” Posachedwa kuthambo kudangoti bii ndi mitambo, mphepo idaomba ndipo padagwa mvula yaikulu. Ahabu adakwera galeta napita ku Yezireele. Mphamvu za Chauta zinali naye Eliya. Iyeyo adakwinda chovala chake, nathamanga mwaliŵiro, nkupitirira Ahabu mpaka adayambira ndiye kukafika ku chipata cha ku Yezireele. Ahabu adauza Yezebele zonse zimene adachita Eliya zija, ndipo kuti adapha aneneri onse a Baala ndi lupanga. Pomwepo Yezebele adatuma munthu kukauza Eliya kuti, “Milungu indilange ngakhale kundipha kumene, ngati sindikupha iweyo maŵa nthaŵi yonga yomwe ino, monga momwe udaphera aneneriwo.” Pamenepo Eliya adachita mantha, ndipo adanyamuka nathaŵa kuti apulumutse moyo wake. Adakafika ku Beereseba, mzinda wa ku Yuda, nakasiya mtumiki wake kumeneko. Koma Eliya mwini wake adayenda ulendo wa tsiku limodzi m'chipululu, nakakhala pansi patsinde pa kamtengo ka tsache. Tsono adapempha kuti afe, adati, “Zandikola! Inu Chauta, bwanji ndingofa basi! Ine sindingapambane makolo anga.” Atatero adagona tulo patsinde pa kamtengo ka tsache pomwepo. Mwadzidzidzi mngelo adamkhudza namuuza kuti, “Dzuka, udye.” Eliya atapenya, adangoona kuti kumutu kwake kuli buledi wootcha pa makala, ndiponso mkhate wa madzi. Adadya, namwera, nkugonanso. Mngelo wa Chauta uja adabweranso kachiŵiri, namkhudza nati, “Dzuka, udye kuti ulendowu ungakukanike.” Eliya uja adadzuka, nadya nkumwera. Motero adapeza mphamvu zoyendera. Adayenda masiku makumi anai usana ndi usiku mpaka adakafika ku Sinai, phiri la Mulungu. Kumeneko adafikira m'phanga, nagona momwemo. Tsono Chauta adadzamuuza kuti, “Ukuchitako chiyani kuno, iwe Eliya?” Eliya adayankha kuti, “Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, ineyo ndakhala ndikutumikira Inu nokha nthaŵi zonse. Koma anthu a ku Israele aphwanya chipangano chimene adachita ndi Inu, ndipo agwetsa maguwa anu ndi kupha aneneri anu ndi lupanga. Ineyo ndangotsala ndekha. Tsono akufunafunanso moyo wanga, kuti andiphe.” Apo Chauta adati, “Tuluka, ukaime pa phiri, pamaso panga.” Tsono Chauta adadutsa pamenepo, ndipo mphepo yamphamvu idaomba ning'amba mapiri ndi kuswa matanthwe, koma Chauta sanali m'mphepomo. Itapita mphepoyo, padachita chivomezi, koma Chauta sanali m'chivomezimo. Chitapita chivomezi chija, padafika moto, koma Chauta sanali m'motomo. Utapita motowo, padamveka kamphepo kongoti wii. Eliya atakamva, adafunda kumutu, ndipo adatuluka, nakaima pa khomo la phanga. Pomwepo padamveka mau omuuza kuti, “Ukuchita chiyani kuno, iwe Eliya?” Iyeyo adati, “Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, ineyo ndakhala ndikutumikira Inu nokha nthaŵi zonse. Koma anthu a ku Israele aphwanya chipangano chimene adachita ndi Inu, ndipo agwetsa maguwa anu ndi kupha aneneri anu ndi lupanga. Ineyo ndangotsala ndekha. Tsono akufunafunanso moyo wanga kuti andiphe.” Apo Chauta adamuuza kuti, “Bwerera, tsata njira yopita ku chipululu cha ku Damasiko. Ukakafika kumeneko, ukadzoze Hazaele kuti akhale mfumu ya ku Siriya. Yehu mwana wa Nimisi ukamdzoze kuti akhale mfumu ya ku Israele. Ndipo Elisa, mwana wa Safati wa ku Abele-Mehola, ukamdzoze kuti akhale mneneri woloŵa m'malo mwako. Tsono amene adzapulumuke ku lupanga la Hazaele, Yehu adzamupha. Amene adzapulumuke ku lupanga la Yehu, Elisa adzamupha. Komabe ku Israele ndasungako anthu zikwi zisanu ndi ziŵiri, omwe sadagwadireko Baala kapena kumpsompsona fano lake.” Eliya atachoka kumeneko, adakapeza Elisa akulima ndi pulawo yokokedwa ndi ng'ombe. Panali magoli khumi ndi aŵiri, mwiniwakeyo nkumakuyenda ndi goli lotsiriza. Eliya adabwera kumene kunali iyeko, namuveka mwinjiro wake. Pomwepo Elisa adasiya ng'ombe zakezo, adathamangira Eliya uja nampempha kuti, “Mundilole kuti ndikatsazike bambo wanga ndi mai wanga, ndipo pambuyo pake ndidzakutsatani.” Eliya adamuyankha kuti, “Chabwino, pita. Ndakuletsa ngati?” Apo Elisa adabwerera, ndipo adatenga ng'ombe zake ziŵiri nazipha. Kenaka adatenga magoli a ng'ombezo nasonkhera moto nkuphikira nyamayo, ndipo adaipereka kwa anthu kuti adye. Pambuyo pake adanyamuka namayenda ndi Eliya ndi kumamtumikira. Benihadadi, mfumu ya ku Siriya, adasonkhanitsa magulu ake onse ankhondo, ndipo adagwirizana ndi mafumu ena 32 okhala ndi akavalo ndi magaleta. Iyeyo ndi mafumu anzakewo adapita ndipo adakazinga mzinda wa Samariya nauthira nkhondo. Tsono Benihadadi adatuma amithenga ake kwa Ahabu mumzindamo kukamuuza mau akuti awapatse amithengawo siliva wake pamodzi ndi golide yemwe. Akazi ake okongola, pamodzi ndi ana omwe. Ahabu, mfumu ya ku Israele, adayankha kuti, “Monga m'mene mbuyanga mfumu akuneneramo, ineyo ndine wake pamodzi ndi zonse zomwe ndili nazo.” Tsono amithenga aja adabweranso kwa Ahabu kachiŵiri ndi mau a Benihadadi onena kuti, “Ndidaakuuza kuti unditumizire siliva wako pamodzi ndi golide wako, akazi ako pamodzinso ndi ana ako omwe. Koma maŵa nthaŵi yonga yomwe ino, ndidzatuma ankhondo anga kumeneko, adzaloŵa m'nyumba zako ndi za nduna zako, ndipo adzatenga zinthu zonse zimene zidzaŵakomere.” Apo mfumu Ahabu adaitana akuluakulu onse am'dzikomo naŵauza kuti, “Tsopano mungathe kuwona kuti munthuyu akufuna kutiwononga ife. Adanditumizira mau akuti ndimpatse akazi anga, ana anga, pamodzi ndi siliva ndi golide yemwe, ndipo ine sindidamkanize.” Akuluakulu onsewo pamodzi ndi anthu omwe adati, “Musasamaleko zimenezo kapena kumuvomereza ai.” Tsono Ahabuyo adauza amithenga a Benihadadi aja kuti, “Mbuyangayo muuzeni kuti, ‘Zonse zimene adanena poyamba paja ndidzachita zimenezo. Koma zatsopano zokhazi sindingathe kuchita.’ ” Amithenga aja adachoka nakauza Benihadadi mau amenewo. Pamenepo Benihadadi adatumizanso mau kwa Ahabu kuti, “Ndibwera ndi anthu anga ambiri kudzaononga mzinda wakowo, ndipo adzausandutsa fumbi lokhalokha. Milungu indilange ngati ndilephera kuchita zimenezi.” Ahabu, mfumu ya ku Israele, adayankha kuti, “Kamuuzeni kuti, ‘Mwamuna mnzako mpachulu, kulinga utakwerapo. Wankhondo weniweni ndi amene amadzitama atapambana, osati asanamenye nkhondo.’ ” Benihadadi adamva mau ameneŵa, pamene ankamwa pamodzi ndi mafumu anzake aja m'mahema, tsono adauza anthu ake aja kuti, “Konzekerani nkhondo.” Ndipo anthuwo adakonzekera kuuthira nkhondo mzindawo. Nthaŵi imeneyo mneneri wina adadza kwa Ahabu, mfumu ya ku Israele, namuuza mau a Chauta akuti, “Kodi ukuchiwona chigulu cha ankhondochi? Ndithudi ndikuchipereka chigulu chimenechi m'manja mwako lero lino. Motero udzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.” Ahabu adafunsa kuti, “Kodi zimenezo zidzachitika ndi yani?” Mneneriyo adati, “Chauta akuti zidzachitika ndi ankhondo a nduna zam'maboma.” Ahabu adafunsanso kuti, “Nanga amene adzayambe nkhondoyo ndani?” Mneneriyo adati, “Iweyo.” Pamenepo Ahabu adasonkhanitsa ankhondo a nduna zam'maboma, ndipo onse pamodzi analipo 232. Pambuyo pake adasonkhanitsanso gulu la ankhondo a ku Israele zikwi zisanu ndi ziŵiri onse pamodzi. Adatuluka masana nthaŵi imene Benihadadi ndi mafumu 32 othandizana nawo aja ankamwa mpaka kuledzera m'mahema mwao. Ankhondo a nduna zam'maboma aja, ndiwo amene adayamba kupita ku nkhondo. Nthaŵi yomweyo Benihadadi adatuma anthu oti akazonde. Iwo adadzamuuza kuti, “Kukubwera ankhondo kuchokera ku Samariya.” Benihadadiyo adauza azondi aja kuti, “Ngati akubwera ndi mtendere, muŵagwire amoyo. Ngatinso akubwera ndi nkhondo, muŵagwirebe amoyo.” Ankhondo a nduna zam'maboma aja adayamba kuthira nkhondo pamodzi ndi gulu la ankhondo a ku Israele limene linkaŵatsata. Aliyense mwa iwowo adapha munthu wake. Asiriya aja adathaŵa, ndipo anthu a ku Israele adaŵalondola, koma Benihadadi, mfumu ya ku Siriya, adapulumuka atakwera kavalo, iye pamodzinso ndi ankhondo ena okwera akavalo. Koma mfumu ya ku Israele idagwira akavalowo pamodzi ndi magaleta omwe, ndipo idagonjetsa Asiriya kotheratu. Pambuyo pake mneneri uja adadzanso kwa Ahabu, mfumu ya ku Israele, namuuza kuti, “Tiyeni, valani chamuna, ndipo muganize bwino zoti mudzachite. Pakuti chaka chikudzachi, mfumu ya ku Siriya idzabweranso kudzamenyana nanu nkhondo.” Kwao kuja akuluakulu a mfumu ya ku Siriya adauza mfumu yao kuti, “Milungu ya anthu a ku Israele ndi milungu yam'mapiri, nchifukwa chake anali ndi mphamvu zotipambanira ife. Koma tiyeni tikamenyane nawo ku chigwa, ndithudi tidzaŵapambana. Tsono muchite izi: chotsani mafumu onse aja pa ulamuliro wao, ndipo m'malo mwao muikemo akuluakulu ankhondo. Kenaka musonkhanitse gulu lankhondo lofanafana ndi gulu lankhondo lidaonongeka lija, akavalo onga omwe aja, ndi magaleta onga omwe ajanso. Pambuyo pake tidzamenyana nawo ku chigwa. Ndithudi, pamenepo tidzaŵapambana.” Benihadadiyo adamvera mau a akuluakulu akewo, ndipo adachitadi momwemo. Pamene chinkafika chaka china chija, Benihadadi adasonkhanitsa gulu lankhondo la Asiriya, napita ku mzinda wa Afeki, kuti akamenyane ndi ankhondo a ku Israele. Anthu a ku Israele adasonkhana, ndipo atalandira zofunikira, adapita kukamenyana ndi Asiriya. Ndiye adamanga zithando zao zankhondo moyang'anana ndi Asiriya ndipo ankangooneka ngati timagulu tiŵiri ta mbuzi, m'menemo Asiriya adaadzaza dera lonselo. Nthaŵiyo munthu wa Mulungu adadza kwa Ahabu, mfumu ya ku Israele, namuuza kuti, “Chauta akunena kuti, ‘Popeza kuti Asiriya akuti Chauta ndi mulungu wakumapiri osati wakuzigwa, ndipereka chigulu chonsechi kwa iwe, ndipo udzadziŵa kuti Ine ndine Chauta!’ ” Apo nkuti anthu a ku Israele ndi a ku Siriya atakhala m'zithando moyang'anana masiku asanu ndi aŵiri. Pa tsiku la chisanu ndi chiŵiri, nkhondo idagundika. Anthu a ku Israele adakantha Asiriya okwanira 100,000 tsiku limodzi lokha, ankhondo apansi okhaokha. Ena otsala adathaŵira ku mzinda wa Afeki, ndipo khoma lidagwa, kugwera pa anthu okwanira 27,000, omwe adatsalawo. Benihadadi nayenso adathaŵa, nakabisala m'chipinda cham'kati mumzindamo. Ndipo akuluakulu ake adamuuza kuti, “Onani tsono, ife tamva kuti mafumu a fuko la anthu a ku Israele ngachifundo. Tiyeni tivale ziguduli m'chiwuno ndi kuzeŵeza zingwe m'khosi, tipite kwa mfumu ya ku Israeleyo, mwina sakakuphani.” Motero adavaladi ziguduli m'chiwuno ndi kuzeŵeza zingwe m'khosi, napita kwa mfumu ya ku Israele, nkukaiwuza kuti, “Mtumiki wanu Benihadadi akunena kuti, ‘Chonde, mundisungire moyo.’ ” Ahabu adaŵafunsa kuti, “Kani akali moyobe? Iye ujatu ndi mbale wanga.” Tsono anthuwo adaganiza kuti mauwo ngabwino, navomera mofulumira kuti, “Inde, Benihadadi ndi mbale wanudi.” Pompo Ahabuyo adati, “Pitani mukamtenge.” Tsono Benihadadi adabweradi ndipo Ahabu adamkweza pa galeta lake. Benihadadi adauza Ahabu kuti, “Mizinda imene bambo wanga adalanda bambo wanu ndidzakubwezerani. Tsono mungathe kumanga nyumba zanu zamalonda ku Damasiko, monga momwe adachitira bambo wanga ku Samariya.” Ahabu adamuuza kuti, “Ukachita zimenezi, ndiye kuti ndidzakulola kuti upite.” Tsono adachita naye chipangano, namlola kuti apite. Tsiku lina munthu wina, mmodzi mwa aneneri, atalamulidwa ndi Chauta, adauza mneneri mnzake kuti, “Iwe, menye ndithu, ndakupemba.” Koma mnzakeyo adakana kummenya. Tsono mneneri uja adati, “Popeza kuti sudamvere mau a Chauta, ukangochoka pano, mkango ukupha.” Ndiyedi atangochoka pamenepo, adakumana ndi mkango, numupha. Tsono mneneriyo adapeza mneneri mnzake winanso, namuuza kuti, “Chonde, undimenye.” Mnzakeyo adammenyadi, namtematema pomumenyapo. Tsono mneneri uja adachokapo, nakadikirira mfumu pa njira, atadzizimbaitsa pokulunga nsalu kumaso. M'mene mfumu inkapita pamenepo, mneneri uja adafuula kuti, “Ine mtumiki wanu ndidapita kukailowerera nkhondo pakati penipeni. Ndipo wankhondo wina anabwera kwa ine atatenga mmodzi mwa adani athu, nanena kuti, ‘Sunga munthu uyu. Akasoŵa mwa njira iliyonse, ndiye kuti ndidzakupha kapena udzalipira ndalama 3,000 zasiliva.’ Pamene ine mtumiki wanu ndinkatanganidwa apa ndi apa, munthuyo adazemba.” Apo Ahabu, mfumu ya ku Israele, adamuuza kuti, “Momwemo ndimo ukhalire mlandu wako. Iweyo wadzitsutsa wekha.” Munthuyo adachotsa msangamsanga nsalu kumaso, ndipo Ahabu adamzindikira kuti ndi mmodzi mwa aneneri. Tsono mneneriyo adamuuza kuti, “Chauta akunena kuti, ‘Poti wamtaya munthu amene Ine ndidati umuphe, ndiye kuti iweyo ndiwe amene udzaphedwe m'malo mwa iyeyo, ndipo anthu ako adzaphedwa m'malo mwa anthu ake.’ ” Motero Ahabu, mfumu ya ku Israele, adabwerera kunyumba kwake mwachisoni ndi mosakondwa, naloŵa mu mzinda wa Samariya. Panali munthu wina wa ku Yezireele dzina lake Naboti. Iyeyo anali ndi munda wamphesa ku Yezireele, pafupi ndi nyumba ya mfumu Ahabu. Tsiku lina, Ahabu adauza Naboti kuti, “Tandipatsa munda wakowu kuti ukhale dimba langa, poti uli pafupi ndi nyumba yanga. M'malo mwake ndidzakupatsa wina wabwino koposa, kapena ngati ufuna, ndidzakupatsa ndalama pa mtengo wake wa mundawo.” Koma Naboti adauza Ahabu kuti, “Ndithu, pali Chauta, sindingakupatseni choloŵa cha makolo anga.” Apo Ahabu adakaloŵa m'nyumba mwake atakwiya, msunamo uli toloo chifukwa cha zimene Naboti wa ku Yezireele adaanena, pakuti adaati, “Sindingakupatseni choloŵa cha makolo anga.” Motero Ahabu adakagona pabedi pake atapenya ku khoma, osafuna ndi kudya komwe. Koma Yezebele, mkazi wake uja, adabwera kwa iye namufunsa kuti, “Chifukwa chiyani nkhope yanu ikuwoneka yosakondwa, ndipo simukufuna chakudya?” Ahabu adauza mkazi wakeyo kuti, “Chifukwa chake nchakuti ine ndinakamba ndi Naboti wa ku Yezireele ndi kumuuza kuti andipatse munda wake wamphesawu kuti ndigule, kapena ngati afuna, ndidzamupatse munda wina m'malo mwake. Koma iyeyo wayankha kuti, ‘Sindidzakupatsani munda wanga wamphesawu.’ ” Apo Yezebele mkazi wakeyo adamufunsa kuti, “Kodi mfumu ya ku Israele sindinu? Dzukani, kadyeni, mtima wanu usangalale. Ine ndidzakutengerani munda wamphesawo kwa Naboti wa ku Yezireele.” Tsono Yezebele adalemba makalata m'dzina la Ahabu, naŵasindikiza ndi chidindo cha mfumu. Adatumiza makalatawo kwa akuluakulu ndi kwa atsogoleri amene ankakhala ndi Naboti mumzinda mwake. M'makalatamo adalembamo kuti, “Lalikani kuti anthu asale zakudya, ndipo Naboti amuike pa malo aulemu. Mupeze anthu aŵiri oipa mtima kuti adzamneneze ndi mau akuti, ‘Iwe watemberera Mulungu ndiponso mfumu.’ Tsono mumtulutsire kunja, ndipo mumponye miyala kuti afe basi.” Motero anthu a mumzinda m'mene ankakhala Nabotiyo, akuluakulu ndi atsogoleri amumzindamo, adachitadi monga momwe adaaŵauzira Yezebele. Potsata mau am'makalata omwe mkaziyo adaŵatumizira, anthuwo adalengeza za kusala zakudya, ndipo adamuika Naboti pa malo aulemu. Anthu aŵiri aja adaloŵa nakhala pamaso pa Nabotiyo. Adayamba akuchita umboni pakhamu pa anthu onse kuti, “Nabotiyu adatemberera Mulungu ndiponso mfumu.” Motero anthuwo adamtulutsira kunja kwa mzinda, namponya miyala mpaka kumupha. Pambuyo pake adatumiza mau kwa Yezebele akuti, “Naboti uja takonza, moti wafa.” Yezebele atangomva zakuti Naboti amponya miyala ndipo wafa, adakauza Ahabu kuti, “Dzukani, katengeni munda wamphesa uja umene Naboti Myezireele, ankakukanizani kugula. Nabotiyo sali moyonso ai, wafa.” Ahabu atangomva kuti Naboti wafa, adanyamuka napita ku munda wamphesa wa Naboti Myezireele, nautenga kuti ukhale wake. Pambuyo pake Chauta adauza Eliya wa ku Tisibe kuti, “Nyamuka, pita ukakumane ndi Ahabu, mfumu ya ku Israele, amene akukhala ku Samariya. Iyeyu ali ku munda wamphesa wa Naboti. Wapita kumeneko kuti akatenge mundawo kuti ukhale wake. Tsono ukamuuze kuti Chauta akukufunsa kuti, ‘Kodi wapha, ndipo walandanso?’ Ukamuuzenso kuti, ‘Chauta akunena kuti, pa malo amene agalu ankanyambita magazi a Naboti, pomweponso agalu adzanyambita magazi ako.’ ” Apo Ahabu adafunsa Eliya kuti, “Kani wandipeza, iwe mdani wanga?” Eliya adayankha kuti, “Ee, ndakupezani, chifukwa inuyo mwadzigulitsa ndi kukhala ngati kapolo wa zoipa zochimwira Chauta. Tsopano Chauta akuti, ‘Ndithu, ndidzakupasula. Ndidzakusesa kwathunthu, ndidzaononga mwamuna aliyense pa banja lako, kapolo kapena mfulu, m'dziko la Israele. Ndipo banja lako ndidzalisandutsa kuti likhale ngati banja la Yerobowamu mwana wa Nebati, ndiponso ngati banja la Baasa mwana wa Ahiya. Nawenso wandikwiyitsa, chifukwa chakuti wachimwitsa anthu a ku Israele’ Tsono kunena za Yezebele, Chauta akuti agalu adzamudya Yezebele m'kati mwa malinga a Yezireele. Munthu aliyense wa banja la Ahabu amene adzafere mu mzinda, agalu adzamudya. Ndipo aliyense wa banja limenelo wodzafera ku thengo, mbalame zamumlengalenga ndizo zidzamudye.” Kunena zoona kunalibe ndi mmodzi yemwe amene adadzipereka ku zoipa kuchimwira Chauta ngati Ahabu, amene Yezebele mkazi wake adamkopa. Iyeyo adachita zonyansa kwambiri popembedza mafano, monga m'mene ankachitira Aamori aja, amene Chauta adaŵachotsa pamene Aisraele ankafika. Ahabu atamva mau amenewo, adang'amba zovala zake, navala ziguduli. Adasala zakudya nagona pa zigudulizo, ndipo adayamba kuyenda modzichepetsa. Apo Chauta adauza Eliya wa ku Tisibe kuti, “Kodi waona m'mene Ahabu wadzichepetsera pamaso panga? Popeza kuti wadzichepetsa pamaso panga, sindidzamlanga ndi zonse zija iyeyo ali moyo. Koma ndidzalanga banja lake, kuyambira mwana wake.” Padapita zaka zitatu popanda nkhondo pakati pa Siriya ndi Israele. Pa chaka chachitatu Yehosafati mfumu ya ku Yuda adakacheza kwa Ahabu, mfumu ya ku Israele. Tsono Ahabu adafunsa aphungu ake kuti, “Ramoti-Giliyadi ndi mzinda wathu, nanga chifukwa chiyani ife tikukhala chete, osaulanda kwa mfumu ya ku Siriya?” Ndipo adafunsa Yehosafati kuti, “Kodi udzapita nane limodzi ku nkhondo ku Ramoti-Giliyadi?” Yehosafati adauza mfumu ya ku Israeleyo kuti, “Ine ndili nanu limodzi, anthu anga nganu, akavalo anga nganunso.” Yehosafati adauza Ahabu kuti, “Poyamba upemphe nzeru kwa Chauta.” Tsono Ahabu adasonkhanitsa aneneri ake okwanira ngati 400, ndipo adaŵafunsa kuti, “Kodi ndipite kukamenyana nkhondo ndi Ramoti-Giliyadi, kaya kapena ndileke?” Aneneriwo adamuuza kuti, “Pitani, pakuti Ambuye aupereka mzindawo kwa inu mfumu.” Koma Yehosafati adafunsa kuti, “Kodi pano palibe mneneri wina wa Chauta woti timpempheko nzeru?” Ahabu adauza Yehosafati kuti, “Alipo munthu wina amene angapemphe nzeru kwa Chauta, dzina lake ndi Mikaya, mwana wa Imila. Koma ine ndimadana naye ameneyo popeza kuti sandilosera zabwino koma zoipa.” Tsono Yehosafati adati, “Iyai mfumu, msatero.” Apo Ahabu adaitana imodzi mwa nduna zake nkuiwuza kuti, “Takaitanani Mikaya, mwana wa Imila, abwere kuno msanga.” Nthaŵi imeneyo mfumu ya ku Israele ndi Yehosafati mfumu ya ku Yuda adaakhala pa mipando yao yaufumu, atavala zovala zao zaufumu. Pamenepo panali pa bwalo lopererapo tirigu, pa khomo la pa chipata cha Samariya. Ndipo aneneri onse ankalosa pamaso pa mafumuwo. Wina mwa iwo, Zedeki, mwana wa Kenana adaadzisulira nyanga zachitsulo. Iyeyo adati, “Chauta akunena kuti, ‘Ndi nyangazi iwe udzagonjetsa Asiriya mpaka kuŵaonongeratu.’ ” Aneneri onsewo adalosa chimodzimodzi, adati, “Pitani ku Ramoti-Giliyadi, ndipo mukapambana. Chauta aupereka mzindawo kwa inu mfumu.” Wamthenga uja amene adaapita kukaitana Mikaya namuuza kuti, “Onani, mau onse amene akunena aneneri, akulosera mfumu zabwino. Ndiye nanunso mau anu akhale ofanafana ndi mau aowo. Muzilosa zabwino.” Koma Mikaya adati, “Pali Chauta wamoyo, zimene Chautayo andiwuze, ndizo ndidzalankhule.” Tsono atafika kwa Ahabu, mfumuyo idamfunsa kuti, “Kodi Mikaya, ife tipite kukamenya nkhondo ku Ramoti-Giliyadi, kapena tileke?” Iye adayankha kuti, “Pitani, mukapambana. Chauta adzaupereka mzindawo kwa inu amfumu.” Koma mfumuyo idamufunsa kuti, “Kodi ndikulumbiritse kangati, kuti undiwuze zoona zokhazokha m'dzina la Chauta?” Mikaya adati, “Ndidaona Aisraele onse atamwazikana pa mapiri ngati nkhosa zopanda mbusa. Tsono Chauta adati, ‘Ameneŵa alibe mbuyawo. Aliyense apite kwao mwamtendere.’ ” Pamenepo mfumu ya ku Israele idafunsa Yehosafati kuti. “Suja ndidaakuuzani kuti ameneyu sadzandilosera zabwino, koma zoipa zokha?” Apo Mikaya adati, “Nchifukwa chake mverani mau a Chauta. Ine ndidapenya Chauta atakhala pa mpando wake waufumu, gulu lonse lakumwamba litaima ku dzanja lake lamanja ndi ku dzanja lake lamanzere. Tsono Chauta adati, ‘Kodi ndani amene akanyengerere Ahabu kuti akafe ku Ramoti-Giliyadi?’ Wina ankanena zina, winanso nkumanena zina. Apo mzimu wina udadzaima pamaso pa Chauta nunena kuti, ‘Ndikamnyengerera ndine.’ Tsono Chauta adaufunsa kuti, ‘Ukamnyengerera bwanji?’ Mzimuwo udati, ‘Ndidzapita nkumakanena zabodza kudzera mwa aneneri ake onse.’ Pamenepo Chauta adati, ‘Ukakatero, ukakhozadi. Pita ukamnyengerere.’ Tsonotu Chauta waika bodza m'kamwa mwa aneneri anu onseŵa, ndiye kuti Iye yemwe waneneratu kuti mukaona tsoka.” Tsono Zedeki uja, mwana wa Kenana, adadza pafupi namenya Mikaya pa tsaya, namufunsa kuti, “Kodi mzimu wa Chauta udadzera njira iti kuti uchoke mwa ine, uzikalankhula ndi iwe?” Mikaya adayankha kuti, “Udzadziŵa pa tsiku limene uzikaloŵa m'chipinda china ndi china cham'kati kuti ukabisale.” Pamenepo Ahabu, mfumu ya ku Israele, adati, “Mgwireni Mikayayu, mupite naye kwa Amoni, mkulu wa mzinda, ndiponso kwa Yowasi, mwana wa mfumu. Mukaŵauze mau angaŵa akuti, ‘Munthu uyu muikeni m'ndende ndipo muzimpatsa chakudya pang'ono ndi madzi pang'ono mpaka nditabwerera mwamtendere.’ ” Mikaya adati, “Mukabwerera mwamtendere, ndiye kuti Chauta sadalankhule kudzera mwa ine.” Ndipo adaonjeza kuti, “Mumve anthu nonsenu zimene ndanenazi!” Zitatero, Ahabu mfumu ya ku Israele ndi Yehosafati mfumu ya ku Yuda adapita ku Ramoti-Giliyadi. Mfumu ya ku Israele idauza Yehosafati kuti, “Ine ndidzizimbaitsa, ndipo ndipita kunkhondoko, koma iwe uvale malaya ako aufumu.” Choncho mfumu ya ku Israele idadzizimbayitsa onsewo nkupita ku nkhondo. Mfumu ya ku Siriya nkuti italamula akapitao a magaleta okwanira 32, kuti asamenye nkhondo ndi wina aliyense, wamng'ono kapena wamkulu, koma mfumu ya ku Israele basi. Tsono pamene akapitao a magaletawo adaona Yehosafati, adati, “Ndithudi ameneyo ndiye mfumu ya ku Israele.” Choncho adabwerera kudzalimbana naye. Yehosafati adayamba kufuula. Apo akapitao a magaleta aja adaona kuti si mfumu ya ku Israele, ndipo adabwerera osamtsatanso. Koma Msiriya wina adakoka uta wake mwachiponyeponye, ndipo adalasa mfumu ya ku Israele pa maluma a malaya ake achitsulo. Pamenepo mfumuyo idauza munthu woyendetsa galeta lake kuti, “Tembenuka, ndipo undichotse pankhondo pano poti ndavulazidwa.” Nkhondo idakula kwambiri tsiku limenelo, mwakuti mfumu ija adangoisiya ili tsonga m'galeta lake atayang'anana ndi Asiriya, mpaka mfumuyo idafa madzulo. Monsemo nkuti magazi akutayikira pansi pa galetalo. Pamene dzuŵa linkaloŵa kudamveka mfuu wa ankhondo kuti, “Aliyense apite ku mzinda wakwao, aliyense apite ku dziko lakwao.” Motero mfumu ija idafa, ndipo anthu adapita nayo ku Samariya, nakaiika m'manda kumeneko. Anthu aja adatsuka galeta lija ku chidziŵe cha ku Samariya, kumene akazi adama ankasamba. Ndipo agalu adayamba kunyambita magazi a mfumuyo, potsata mau amene Chauta adaalankhula. Tsono ntchito zina za Ahabu ndi zonse zimene adazichita, kudzanso za nyumba ya minyanga ya njovu yomwe adaimanga, ndiponso za mizinda yonse imene adaimanga, zonsezo zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele. Choncho Ahabu adamwalira, kulondola makolo ake naikidwa m'manda. Ahaziya mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Yehosafati, mwana wa Asa, adayamba kulamulira ku Yuda pa chaka chachinai cha ufumu wa Ahabu, mfumu ya ku Israele. Yehosafatiyo anali wa zaka 35 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 25 ku Yerusalemu. Mai wake anali Azuba, mwana wa Sili. Yehosafati ankayenda motsata chitsanzo chabwino cha atate ake. Sadapatuke pa zimenezo. Ankachita zolungama pamaso pa Chauta. Komabe akachisi opembedzerako mafano sadaŵawononge, mwakuti anthu ankaperekabe nsembe ndipo ankafukizabe lubani pa malowo. Chinanso nchakuti Yehosafati adapangana za mtendere ndi mfumu ya ku Israele. Tsono ntchito zina zonse za Yehosafati, mphamvu zimene adaonetsa, ndiponso maponyedwe ake a nkhondo, zonsezo zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda. Chinanso ndiye kuti Yehosafati adapirikitsa gulu lotsalira la anthu ochitana zadama ku malo achipembedzo, amene anali adakalipo pa nthaŵi ya Asa, bambo wake. Masiku amenewo ku Edomu kunalibe mfumu, koma kunali nduna yaikulu chabe yoikidwa ndi mfumu ya ku Yuda. Tsono Yehosafati adapanga zombo zazikulu zomapita ku Ofiri kukatenga golide. Koma zombozo sizidayende chifukwa zidaaonongeka ku Eziyoni-Gebere. Tsono Ahaziya mwana wa Ahabu, adauza Yehosafati kuti, “Amalinyero anga apite limodzi ndi amalinyero anu pa zombo.” Koma Yehosafati sadavomere zimenezi. Pambuyo pake Yehosafati adamwalira, naikidwa m'manda momwe adaaikidwa makolo akewo mu mzinda wa Davide. Ndipo Yehoramu mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Tsono Ahaziya mwana wa Ahabu, adaloŵa ufumu wa Ku Israele ku Samariya pa chaka cha 17 cha ufumu wa Yehosafati, mfumu ya ku Yuda. Ndipo adalamulira anthu a ku Israele zaka ziŵiri. Iyeyo ankachita zoipa pamaso pa Chauta, ankatsata mayendedwe oipa a atate ake ndi amai ake. Ankatsatanso zoipa za Yerobowamu, mwana wa Nebati, amene ankachimwitsa kwambiri anthu a ku Israele. Ahaziyayo ankatumikira Baala ndi kumampembedza, ndipo potero adaputa mkwiyo wa Chauta, Mulungu wa Aisraele, potsata zonse zimene atate ake ankachita. Atamwalira mfumu Ahabu, Amowabu adaukira Aisraele. Tsiku lina mfumu Ahaziya ali ku likulu lake ku Samariya, adagwa kuchokera pa khonde la chipinda chake cham'mwamba, navulala kwambiri. Ndiye adatuma amithenga naŵauza kuti, “Pitani, mukafunse kwa Baala-Zebubi, mulungu wa anthu a ku Ekeroni, ngati nditi ndichire.” Koma mngelo wa Chauta adauza mneneri Eliya wa ku Tisibe kuti, “Nyamuka, pita ukakumane ndi amithenga a mfumu ya ku Samariya, ukaŵafunse kuti, ‘Kodi ku Israele kulibe Mulungu, apa mukupita kukapempha nzeru kwa Baala-Zebubi, mulungu wa anthu a ku Ekeroni?’ Nchifukwa chake tsono mau a Chauta oti mukauze mfumu ndi aŵa: ‘Iweyo sudzuka pabedi wagonapo, koma ufa ndithu.’ ” Ndipo Eliya adapita. Amithenga aja adabwerera kwa mfumu. Tsono mfumuyo idaŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mwabwerera?” Amithengawo adayankha kuti, “Kudaabwera munthu kudzakumana nafe, ndipo adatiwuza kuti, ‘Bwererani kwa mfumu imene idakutumaniyo, mukaiwuze mau a Chauta akuti, “Kodi ku Israele kulibe Mulungu, apa mukukapempha nzeru kwa Baala-Zebubi, mulungu wa anthu a ku Ekeroni? Nchifukwa chake sudzuka pabedi wagonapo, koma ufa ndithu.” ’ ” Tsono mfumuyo idafunsa amithengawo kuti, “Kodi munthu amene adaabwera kudzakumana nanuyo, namakuuzani zimenezi, ankaoneka bwanji?” Iwowo adayankha kuti, “Munthuyo adaavala zovala zaubweya ndi lamba wachikopa m'chiwuno.” Apo mfumuyo idati, “Ameneyo ndi Eliya wa ku Tisibe.” Pomwepo mfumuyo idatuma mkulu wina wa ankhondo ndi anthu ake makumi asanu kukagwira Eliya. Mkuluyo adapita kwa Eliya nampeza atakhala pansi pamwamba pa phiri. Adamuuza kuti, “Inu, munthu wa Mulungu, mfumu ikukulamulani kuti mutsike.” Koma Eliya adauza mkulu wa ankhondo makumi asanu aja kuti, “Ngati ine ndinedi munthu wa Mulungu, moto utsike kumwamba, ukupsereze iweyo pamodzi ndi anthu ako makumi asanuŵa.” Pomwepo moto udatsikadi kumwamba, nupsereza mkuluyo pamodzi ndi anthu ake makumi asanuwo. Tsono mfumu idatumanso mkulu wina pamodzi ndi ankhondo ake makumi asanu. Mkuluyo ndi anthu ake adapita, nakauza Eliya uja kuti, “Inu munthu wa Mulungu, mfumu ikukulamulani kuti mutsike msanga.” Koma Eliya adamuyankha kuti, “Ngati ine ndinedi munthu wa Mulungu, moto utsike kumwamba, ukupsereze iweyo pamodzi ndi anthu ako makumi asanuŵa.” Pomwepo moto wa Mulungu udatsikadi kumwamba, nupsereza mkuluyo pamodzi ndi anthu ake makumi asanu aja. Mfumu ija idatumanso mkulu wina wachitatu pamodzi ndi ankhondo ake makumi asanu. Koma mkulu wachitatu uja adapita nakagwada pamaso pa Eliya, nampempha kuti, “Inu munthu wa Mulungu, chonde ndikukupemphani kuti musandiwononge ineyo pamodzi ndi anthu anga makumi asanuŵa. Onani, moto udatsika kumwamba nupsereza anzanga aja, pamodzi ndi anthu ao omwe. Chonde tipulumutseni, musatiwononge.” Apo mngelo wa Chauta adauza Eliya kuti, “Pita naye, usamuwope.” Tsono Eliya adanyamuka natsika limodzi ndi mkulu uja, kupita kwa mfumu. Ndipo Eliya adauza mfumuyo kuti “Chauta akunena kuti, ‘Pamene udaatuma amithenga kwa Baala-Zebubi, mulungu wa anthu a ku Ekeroni, kodi ndiye kuti kuno ku Israele kulibe Mulungu woti nkumpempha nzeru?’ Nchifukwa chake Chauta akuti, ‘Iweyo sudzuka pabedi wagonapo, koma ufa ndithu.’ ” Motero Ahaziya adafadi potsata mau amene Chauta adaalankhula kudzera mwa Eliya. Ndipo popeza kuti Ahaziya adaalibe mwana wamwamuna, Yoramu mbale wake adaloŵa ufumu m'malo mwake, pa chaka chachiŵiri cha ufumu wa Yehoramu, mwana wa Yosafati, mfumu ya ku Yuda. Tsono ntchito zina za Ahaziya pamodzi ndi zonse zimene adazichita zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a Aisraele. Idafika nthaŵi imene Chauta adafuna kutenga Eliya m'kamvulumvulu kunka kumwamba. Tsiku limenelo Eliya ndi Elisa anali pa ulendo kuchokera ku Giligala. Eliya adauza Elisa kuti, “Iwe, Elisa, chonde ubaakhala pano, poti ine Chauta wandituma kuti ndipite ku Betele.” Koma Elisa adati, “Pali Chauta wamoyo, ndiponso pali inu nomwe, ine sindikusiyani konse.” Motero aŵiri onsewo adapita ku Betele. Tsono a m'gulu la aneneri amene anali ku Beteleko adadzakumana ndi Elisa, namufunsa kuti, “Kodi mukudziŵa kuti lero Chauta akulandani mbuyanu?” Elisa adayankha kuti, “Inde, ndikudziŵa, koma musakambe za zimenezi.” Tsiku lomwelo Eliya adauza Elisa kuti, “Iwe, Elisa, chonde ubaakhala pano, poti ine Chauta wandituma kuti ndipite ku Yeriko.” Koma Elisa adati, “Pali Chauta wamoyo, ndiponso pali inu nomwe, ine sindikusiyani konse.” Motero aŵiri onsewo adakafika ku Yeriko. Ndipo a m'gulu la aneneri amene anali ku Yeriko adadzakumana ndi Elisa, namufunsa kuti, “Kodi mukudziŵa kuti lero Chauta akulandani mbuyanu?” Elisa adayankha kuti, “Inde, ndikudziŵa, koma musakambe za zimenezi.” Pambuyo pake Eliya adauza Elisa kuti, “Iwe, chonde ubaakhala pano, poti ine Chauta wandituma kuti ndipite ku Yordani.” Koma Elisa adauza Eliyayo kuti, “Pali Chauta wamoyo, ndiponso pali inu nomwe, ine sindikusiyani konse.” Motero aŵiri onsewo adapitiriza ulendo wao. Anthu makumi asanu a m'gulu la aneneri aja adapita nawo ndipo adakaimirira chapatali potero, pamene Eliya ndi Elisa adaakaima pa gombe la mtsinje wa Yordani. Apo Eliya adatenga mwinjiro wake naupinda, kenaka adamenya madzi ndi mwinjirowo. Tsono madziwo adapatukana, ena kwina ena kwina, mpaka aneneri aŵiriwo adaoloka pouma. Ataoloka, Eliya adauza Elisa kuti, “Undipemphe choti ndikuchitire ndisanakusiye.” Elisa adati, “Ndikukupemphani kuti ndilandire chigawo chachikulu cha mphamvu zanu za uneneri.” “Eliya adauza Elisayo kuti, ‘Wapempha chinthu chapatali. Komabe ukandipenya pa nthaŵi imene ndikukusiya, zimene wapemphazi zidzakuchitikiradi. Koma ukapanda kundipenya, sizidzachitika.’ ” Tsono iwowo akuyendabe ndi kumakamba, adangoona galeta lamoto ndi akavalo ake amoto zikuŵasiyanitsa aŵiriwo. Ndipo Eliya adakwera kumwamba m'kamvulumvulu. Elisa adaona zimenezi nafuula kuti, “Bambo wanga, Bambo wanga! Magaleta a Aisraele ndi anthu ake okwera pa akavalo.” Ndipo sadamuwonenso Eliyayo. Tsono Elisa adagwira zovala zake nazing'amba paŵiri. Kenaka adatenga mwinjiro wa Eliya umene udaagwa, nabwerera nkukaima pa gombe la Yordani. Adagwira mwinjiro wa Eliyawo namenya nawo madzi aja, nati, “Ali kuti Chauta, Mulungu wa Eliya?” Atamenya madziwo choncho, madzi aja adapatukana, ena kwina, ena kwina. Ndipo Elisa adaoloka. Pamene a m'gulu la aneneri amene ankakhala ku Yeriko adaona Elisayo akuwoloka, adati, “Mphamvu ndi nzeru za Eliya zaloŵa mwa Elisa.” Tsono adabwera kudzakumana naye, namgwadira Elisayo, nkuŵeramitsa mitu yao pansi. Ndipo iwo adamuuza kuti, “Taonani tsono, ife atumiki anu tili ndi anthu amphamvu makumi asanu. Chonde mulole kuti anyamuke akamufunefune mbuyanu Eliya. Mwina mwake mzimu wa Chauta wamtenga nkukamponya kuphiri kwina kapena ku chigwa.” Elisayo adati, “Iyai musaŵatume.” Koma adamkakamiza mpaka Elisayo mwamanyazi adaŵalola naŵauza kuti, “Chabwino, atumeni.” Ndiye iwo adaŵatuma anthu makumi asanuwo. Ndipo anthuwo adakafunafuna Eliya masiku atatu, koma osampeza. Tsono adabwerera kwa Elisayo pamene iyeyo ankadikira ku Yeriko, ndipo iye adaŵauza kuti, “Kodi suja ndidaanena kuti musapite?” Tsiku lina anthu amumzinda adauza Elisa kuti, “Onani, mzinda wathuwu ngwabwino kwambiri, zonse zili bwino monga mukuwoneramu, koma madzi okha ngoipa, ndipo nthaka yake njosabereka.” Apo Elisa adati, “Patseni mbale yatsopano, ndipo muikemo mchere.” Anthuwo adabweradi ndi mchere m'mbale. Tsono Elisa adapita ku kasupe wa madzi, nathiramo mchere m'kasupemo, nati, “Chauta akunena kuti, ‘Madzi ameneŵa ndaŵakonza. Kuyambira tsopano mpaka m'tsogolo, m'madzi ameneŵa simudzakhala chinthu chopha anthu kapena choletsa nthaka kubereka.’ ” Motero madziwo ngabwinobe kwambiri mpaka lero lino, potsata mau amene Elisa adaalankhula. Kuchokera kumeneko Elisa adapita ku Betele. Ndipo pamene anali pa njira, anyamata ena amumzindamo adatuluka nayamba kumseka kuti, “Choka apa, chidazi! Choka apa, chidazi!” Tsono Elisayo adatembenuka, ndipo ataŵaona anyamatawo, adaŵatemberera m'dzina la Chauta. Pompo padatuluka zimbalangondo ziŵiri zazikazi kuchokera kuthengo, nkuphapo anyamata 42. Atachoka kumeneko, Elisa adapitirira kunka ku phiri la Karimele, ndipo pochoka kumeneko adabwerera ku Samariya. Chaka cha 18 cha ufumu wa Yehosafati m'dziko la Yuda, Yoramu mwana wa Ahabu, adaloŵa ufumu wa ku Israele ku Samariya, ndipo adalamulira zaka khumi ndi ziŵiri. Yoramu ankachimwira Chauta, koma kuipa kwake sikudafanefane ndi kwa bambo wake ndi kwa mai wake Yezebele. Yoramuyo adagumula fano la Baala limene bambo wake adaamanga. Komabe adaumirira kuchita zoipa zomwe ankachita Yerobowamu, mwana wa Nebati, zimene adaachimwitsa nazo Aisraele, osafuna konse kuzileka. Kale Mesa, mfumu ya Amowabu, ankaŵeta nkhosa. Ndipo chaka ndi chaka ankapereka ngati msonkho kwa mfumu ya Israele anaankhosa okwanira 100,000, ndiponso ubweya wa nkhosa zamphongo 100,000. Koma Ahabu atamwalira, mfumu ya Amowabuyo idagalukira mfumu ya ku Israele. Motero mwamsangamsanga mfumu Yoramu adatuluka kuchoka ku Samariya, nasonkhanitsa gulu lonse la ankhondo la Aisraele. Kenaka Yoramuyo adatumiza mau kwa Yehosafati, mfumu ya ku Yuda, kuti, “Mfumu ya Amowabu yandigalukira ine. Kodi sungapite nane kunkhondo, kuti tikamenyane ndi Amowabu?” Tsono Yehosafatiyo adayankha kuti, “Ndidzapita. Ine ndi iwe ndife amodzi, anthu anga ndi ako omwe, akavalo anga ndi akonso.” Tsono Yehosafatiyo adafunsa kuti, “Kodi tidzere njira iti popita kunkhondoko?” Yoramu adayankha kuti, “Tidzere ku chipululu cha Edomu.” Motero mfumu ya ku Israele pamodzi ndi mfumu ya ku Yuda kudzanso mfumu ya ku Edomu, onsewo adapita limodzi. Ndipo atayenda mozungululira m'chipululu masiku asanu ndi aŵiri, kunalibe madzi oti amwe asilikali pamodzi ndi nyama zosenza katundu. Tsono mfumu Yoramu adati, “Kalanga ine! Chauta waitana mafumu atatufe, kuti atipereke m'manja mwa Amowabu.” Apo mfumu Yehosafati adafunsa kuti, “Kodi kuno kulibe mneneri woti angatithandize kupempha nzeru kwa Chauta?” Mmodzi mwa atsogoleri a gulu la ankhondo la mfumu Yoramu adayankha kuti, “Aliko Elisa, mwana wa Safati, amene anali mtumiki wa Eliya.” Pomwepo Yehosafati adati, “Elisayo ndiye mneneri weniweni wa Chauta.” Choncho mafumu atatu aja adapita kwa mneneri Elisa. Tsono Elisa adafunsa mfumu Yoramu kuti “Inu kwanga kuno mwadzatani? Bwanji osapita kwa aneneri amene bambo wanu ndi mai wanu ankapemphako nzeru.” Koma Yoramu adati, “Iyai, pakuti Chauta ndiye amene waitana mafumu atatufe, kuti atipereke m'manja mwa Amowabu.” Elisa adati, “Pali Chauta Wamphamvuzonse wamoyo, amene ndimamtumikira, pakadapanda kuti ndimamchitira ulemu Yehosafati mfumu ya ku Yuda, sindikadakusamalani ngakhale kukuyang'anani komwe. Koma tsono mundiitanire munthu wodziŵa kuimba bwino zeze.” Woimba zezeyo atabwera, adaimba nyimbo ndipo mphamvu za Chauta zidadza pa Elisayo. Tsono adati, “Chauta akuti, ‘Mukumbe migwere mu mtsinje wopanda madziwu, ndipo Ine ndidzadzazamo madzi. Simudzaona mphepo kapena mvula, komabe mtsinje wopanda madziwu udzadzaza ndi madzi, ndipo inuyo mudzamwa, pamodzi ndi ng'ombe zanu ndi zoŵeta zanu zina zomwe.’ Koma zimenezi nzochepa kwa Chauta. Iye adzaperekanso Amowabu m'manja mwanu. Mudzagonjetsa mizinda yao yonse yamalinga ndi yabwinoyabwino ija. Mudzagwetsa mitengo yabwino yonse ndi kutseka akasupe onse a madzi, ndipo mudzaononga minda yao yonse yachonde, pakuponyamo miyala.” M'maŵa mwake, nthaŵi yopereka nsembe ili pafupi, adangoona madzi akutuluka kuchokera ku Edomu, mpaka malowo adadzaza madzi. Tsono Amowabu atamva kuti mafumu atatu abwera kuti achite nawo nkhondo, adaitana onse amene ankatha kumenya nkhondo kuyambira wamng'ono mpaka wamkulu. Onsewo adakandanda ku malire. Amowabuwo atadzuka m'mamaŵa pamene dzuŵa linkaŵala pa madzi, adaona madzi ali psuu ngati magazi kutsogolo kwao. Tsono adati, “Taonani magazi! Mafumu aja amenyana okhaokha, ndipo ankhondo ao aphana. Tiyeni tikafunkhe.” Koma Amowabu aja atafika ku zithando za Aisraele, Aisraelewo adaŵathira nkhondo, iwowo nkuyamba kuthaŵa. Koma Aisraele aja ankapha Amowabuwo akuŵapirikitsa. Tsono Aisraele adagumula mizinda yao, ndipo pa munda uliwonse wachonde aliyense ankaponyapo mwala, mpaka minda yonse idadzaza ndi miyala. Adatseka akasupe onse, nagwetsa mitengo yonse yabwino. Kudatsala mzinda wa Kiri-Haresefi wokha, koma pambuyo pake ankhondo oponya miyala adabwera naugonjetsa. Mfumu ya Amowabu itaona kuti nkhondo yaŵaipira, idatenga anthu 700 amalupanga, kuti athaŵe modutsa ankhondo kupita kwa mfumu ya ku Edomu, koma adalephera. Choncho idatenga mwana wake wachisamba amene adaayenera kudzaloŵa ufumu wake, nimpereka pa linga ngati nsembe yopsereza kwa mulungu wa Amowabu. Zimenezi zidadzetsa ukali waukulu wokwiyira Aisraele, mwakuti iwo adangoithaŵa mfumuyo, nabwerera ku dziko lakwao. Tsiku lina mkazi wa mmodzi wa m'gulu la aneneri adapita kwa Elisa. Adampempha mokweza kuti, “Mwamuna wanga, amene anali mtumiki wanu, adamwalira. Ndipo inu mukudziŵa kuti mtumiki wanuyo ankaopa Chauta. Tsono kwafika munthu amene mwamuna wanga adakongola zinthu zake, ndipo akuti atenge ana anga aŵiri, kuti akhale akapolo ake chifukwa cha ngongoleyo.” Elisa adafunsa maiyo kuti, “Nanga mukuti ineyo nditani? Tanenani, muli ndi chiyani m'nyumba mwanu?” Maiyo adayankha kuti, “Mdzakazi wanune ndilibe nkanthu komwe m'nyumba, koma kambiya ka mafuta basi.” Apo Elisayo adamuuza kuti, “Pitani, kabwerekeni mitsuko yambirimbiri kwa anzanu. Mukaloŵe m'nyumba mwanu, mukadzitsekere momwemo inuyo ndi ana anuwo. Ndipo mukatsanyulire mafuta m'mbiya zonsezo. Ina ikadzaza, mukaiike pambali.” Mai uja adachoka kwa Elisayo, nakadzitsekera ndi ana ake aŵiri aja. Tsono iyeyo ankati akathira mafuta m'mbiya nidzaza, ana ake ankabwera ndi mbiya ina. Mbiyazo zitadzaza zonse, maiyo adauza mwana wake kuti, “Bwera ndi inanso mbiya.” Koma mwanayo adauza mai wake kuti, “Palibenso ina.” Pomwepo mafuta aja adaleka kutuluka m'kambiya kaja. Tsono mai uja adapita kukafotokozera Elisa, munthu wa Mulungu uja. Ndipo Elisayo adauza maiyo kuti, “Mai, pitani mukagulitse mafutawo, ndipo mukabweze ngongole zanuzo. Tsono ndalama zotsala zikhale zothandizira inu ndi ana anu.” Tsiku lina Elisa adapita ku Sunemu kumene kunkakhala mai wina wachuma. Maiyo adaumiriza Elisayo kuti adye chakudya kunyumba kwake. Motero Elisa ankati akamadzera njira imeneyo, nthaŵi zonse ankapatuka kunyumbako nkukadya nao. Tsono maiyo adauza mwamuna wake kuti, “Tsopano ndikudziŵa kuti munthu amene amadutsa pano kaŵirikaŵiriyu ngwoyera wa Mulungu. Tiyeni timmangire kachipinda kakang'ono kam'mwamba, ndipo timuikiremo bedi, tebulo, mpando ndi nyale, kuti nthaŵi zonse akatichezera, azitha kumakakhala m'menemo.” Tsiku lina Elisa uja adafika ku Sunemu, nakaloŵa m'kachipinda kam'mwamba kaja kuti akapumule m'menemo. Pambuyo pake adauza mtumiki wake Gehazi kuti aitane maiyo. Gehazi adamuitana maiyo, ndipo adafika kwa Elisa. Elisa adalamula Gehazi kuti amuuze maiyo kuti, “Ndithu mwavutika potichitira zonsezi. Nanga ife tikuchitireni chiyani? Kodi muli ndi mau oti tikakunenereni kwa mfumu, kapena kwa mtsogoleri wankhondo?” Maiyo adayankha kuti, “Ine ndimakhala mwaufulu pakati pa anthu a mtundu wanga.” Ndipo Elisa adafunsanso Gehazi kuti, “Nanga tsono timchitire chiyani?” Gehazi adayankha kuti, “Pepani, mai ameneyu alibe mwana wamwamuna, ndipo mwamuna wake ngwokalamba.” Elisa adati, “Tamuitananso.” Ndipo atamuitana, maiyo adaima pa khomo. Tsono Elisa adauza mai uja kuti, “Pa nthaŵi yonga yomwe ino chaka chamaŵachi, mudzakhala mukululuza mwana wamwamuna.” Ndipo maiyo adati, “Pepani mbuyanga, inu munthu wa Mulungu, musandinamizetu ine mdzakazi wanu.” Koma mai uja adaimadi ndipo chaka chotsatira, nthaŵi ngati yomweyo, adabala mwana wamwamuna, monga momwe Elisa adaamuuzira. Mwana uja atakula, tsiku lina adapita kwa bambo wake amene ankayang'anira anthu odula tirigu. Mwadzidzidzi mwanayo adalira mofuula kwa bambo wake kuti, “Mayo! Mutu wanga ine! Mutu wanga ine!” Bambo wake uja adauza wantchito wake kuti, “Kampereke kwa mai wake.” Adamunyamula, nakampereka kwa mai wake. Mwanayo adakhala pamiyendo pa mai wake mpaka masana, basi nkumwalira. Pomwepo mkazi uja adanyamula mwana wake nakwera ku chipinda cham'mwamba chija, nakamgoneka pa bedi la Elisa, mtumiki wa Mulungu uja, nkumtsekera momwemo, iye nkutuluka. Tsono adaitanitsa mwamuna wake, namuuza kuti, “Tumizireni wantchito mmodzi ndi bulu mmodzi, kuti ndithamangire kwa munthu wa Mulungu uja, nkubwerakonso.” Apo mwamuna wakeyo adafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukupita kwa iyeyo lero? Lerotu si tsiku lokhala mwezi, kapenanso tsiku la Sabata ai.” Mai uja adati, “Palibe kanthu.” Pompo maiyo adaika chishalo nakwera bulu, ndipo adauza wantchitoyo kuti, “Thamangitsa buluyo. Usaleze mpaka ntakuuza.” Motero adayenda nakafika kwa Elisa, munthu wa Mulungu uja, ku phiri la Karimele. Tsono mneneri Elisa ataona kuti mai uja akudza, adauza Gehazi mtumiki wake kuti, “Taona patsidyapo, Msunamu uja akubwera. Thamanga msanga ukamchingamire, ndipo ukamufunse kuti, ‘Kodi nkwabwino? Kodi mwamuna wanu ali bwino? Nanga mwana uja ali bwino?’ ” Mkaziyo adayankha Gehazi kuti, “Inde, nkwabwino.” Tsono atafika kuphiriko kwa Elisa munthu wa Mulungu uja, maiyo adagwada, nagwira mapazi a Elisa. Gehazi adadza kuti amkankhe. Koma Elisa adati, “Mleke, kodi sukuwona kuti ali pa mavuto aakulu? Chauta wandibisira ine zimenezi, sadandiwuze.” Tsono mkaziyo adati, “Kodi inu mbuyanga, ine ndidaakupemphani mwana? Kodi suja ndidaakuuzani kuti musandinamize?” Elisa adauza Gehazi kuti, “Vala lamba wako, fulumira, utenge ndodo yanga ndipo upite. Ukakumana ndi munthu wina aliyense pa njira, usampatse moni, ndipo wina aliyense akakupatsa moni, usayankhe. Tsono ukagoneke ndodo yangayi pa nkhope ya mwanayo.” Apo mai wake wa mwana uja adati, “Pali Chauta wamoyo, ndiponso pali inu nomwe, ine ndiye sindikusiyani ai.” Tsono Elisa adanyamuka natsatira maiyo. Gehazi adatsogolako, ndipo adakaigoneka ndodoyo pa nkhope ya mwana uja, koma sipadamveke mau kapena kuwoneka chizindikiro china cha moyo. Choncho Gehaziyo adangobwerera kukakumana ndi Elisa, ndipo adamuuza kuti, “Mwana uja sadauke ai.” Elisa ataloŵa m'chipinda muja adaona mwana wakufayo atamgoneka pabedi pake. Motero adatseka chitseko nkukhala okha aŵiriwo, ndipo adayamba kupemphera kwa Chauta. Tsono adakamgonera mwanayo, nakhudzitsa pakamwa pake ndi pakamwa pa mwanayo. Ndipo m'mene ankadzitambalitsa choncho pa mwanayo, thupi la mwana uja lidayamba kufunda. Elisayo adadzuka nayenda kamodzi cha uku ndi uku m'chipindamo. Kenaka adakamgoneranso mwana uja, ndipo mwanayo adayetsemula kasanunkaŵiri, nkuphenyula maso. Pomwepo Elisa adaitana Gehazi nati, “Muitane mai uja.” Iye adamuitana maiyo. Ndipo atabwera, Elisayo adati, “Nayu mwana wanu.” Pamenepo maiyo adagwada pa mapazi a Elisa, naŵeramitsa mutu wake pansi. Kenaka adanyamula mwana wake uja, natuluka pa bwalo. Pambuyo pake Elisa adabwereranso ku Giligala, ndipo m'dzikomo munali njala. Tsiku lina Elisa ankaphunzitsa gulu la aneneri, ndipo patapita nthaŵi, adauza mtumiki wake kuti, “Ikapo nkhali yaikulu pa moto, uŵaphikire chakudya a m'gulu la aneneriŵa.” Mmodzi mwa aneneriwo adapita ku thengo kukathyola ndiwo. Kumeneko adakapezako mpesa wakuthengo nathyola zipatso zake kudzaza nsalu yake. Adabwera nazo naziduladula, nkuziika m'nkhali muja, osadziŵa kuti nchiyani. Tsono adapakula naŵapatsa anthuwo kuti adye. Koma pamene adayamba kudya chakudyacho, anthuwo adafuula kuti, “Inu, munthu wa Mulungu, muli dziphe m'nkhalimu.” Choncho sadathe kudya chakudyacho. Tsono Elisa adaŵauza kuti, “Bwerani ndi ufa.” Elisayo adathira ufawo m'nkhali nati, “Apakulireninso anthu chakudyacho kuti adye.” Ndipo adapeza kuti munalibenso zoopsa m'nkhali muja. Tsiku lina munthu wina wochokera ku Baala-Salira adabwera kwa Elisa atamtengerako buledi wopangidwa ndi zokolola zatsopano, mitanda makumi aŵiri ya buledi wa barele ndiponso ngala zatirigu zatsopano. Zonsezi adaazitengera m'thumba mwake. Tsono Elisa adati, “Agaŵire anthu chakudyachi kuti adye.” Koma wantchito wake adamufunsa kuti, “Kodi chakudya chimenechi ndingachigaŵe motani kwa anthu 100 onseŵa?” Elisayo adanenanso kuti, “Apatseni anthuwo, pakuti Chauta akunena kuti, ‘Anthuwo adzadya ndipo chakudyacho chidzatsalako.’ ” Motero wantchitoyo adaŵagaŵira anthuwo chakudyacho, naadya, ndipo adasiyako, monga momwe Chauta adaanenera. Panali mkulu wina wa gulu lankhondo la mfumu ya ku Siriya, dzina lake Naamani, amene anali munthu wokhulupirika kwambiri kwa mbuye wake. Mbuye wakeyo ankamkonda Naamaniyo kwambiri, chifukwa choti ankhondo ake ankapambana pa nkhondo, popeza kuti Chauta anali naye Naamaniyo. Naamaniyo anali munthu wamphamvu ndiponso wolimba mtima, koma anali wakhate. Nthaŵi ina Asiriya adaagwirako mtsikana ku dziko la Israele kumene adakathirako nkhondo, ndipo mtsikanayo adasanduka mdzakazi wa mkazi wa Naamani. Tsono mtsikana uja adauza mkazi wa Naamani kuti, “Bwanji kodi osati ambuyanga apite kwa mneneri ku Samariya, kuti mneneriyo akaŵachize khate laoli.” Naamani atamva zimene adaanena mtsikana uja, adapita kwa mfumu nakaiuza kuti, “Mtsikana amene tidakagwira ku Israele uja wanena kuti ati ndipite ku Samariya, kuti mneneri wakumeneko akandichize.” Pamenepo mfumuyo idamuuza kuti, “Ai ndithu upite, ine ndilemba kalata yofotokozera kwa mfumu ya ku Israele.” Choncho Naamani adanyamuka ulendo wopita ku Samariya, atatenga ndalama zasiliva 30,000, ndalama zagolide 6,000, ndiponso zovala khumi zapachikondwerero. Atafika kwa mfumu ya ku Israele, adapereka kalata ija imene mau ake anali akuti, “Landirani kalatayi. Tsono amene ndakutumiziraniyo ndi Naamani mtumiki wanga, ndipo ndikufuna kuti inuyo mumchize khate lake.” Koma mfumu ya ku Israele ija itaŵerenga kalatayo, idang'amba zovala zake chifukwa cha chisoni, ndipo idati, “Kodi ine ndine Mulungu amene amapha ndi kupatsanso moyo, kuti munthu ameneyu azindilembera mau oti ndichize khate la munthu wake? Nchodziŵikiratu kuti iyeyo akungofuna chifukwa choti ayambane nane.” Koma mneneri Elisa atamva kuti mfumu ya ku Israele idang'amba zovala zake, adatumiza mau kwa mfumuyo akuti, “Chifukwa chiyani mwang'amba zovala zanu? Alendowo abwere kwa ine tsopano lino, kuti adziŵe kuti ku Israele kuli mneneri.” Motero Naamani adadza ndi akavalo ake ndi magaleta ake, nakaima pakhomo pa nyumba ya Elisa. Tsono Elisa adamtumira wamthenga kukamuuza kuti, “Pitani mukasambe mu mtsinje wa Yordani kasanunkaŵiri, ndipo muchira ndi kuyeretsedwa.” Koma Naamani atamva zimenezi, adakwiya kwambiri nachokapo. Popita iye ankati, “Ha! Ine ndimaganiza kuti atuluka kubwera pano, ndipo aimirira natama dzina la Chauta Mulungu wake mopemba, naweyula dzanja lake pamwamba pa nthendapo, ndi kundichiritsa motero. Kodi Abana ndi Faripara, mitsinje ya ku Damasiko, siposa mitsinje yonse ya ku Israele kuno? Monga sindikadatha kukasamba m'mitsinje imeneyo ndi kuchiritsidwa?” Pomwepo adapotoloka, nachokapo molunda. Koma atumiki ake adasendera pafupi namufunsa kuti, “Pepani bambo, kodi mneneri akadakulamulani chinthu chachikulu, inu simukadachita? Monga nchapatali kukasamba monga momwe mneneriyo wakuuziranimo?” Motero Naamaniyo adapita ku Yordani, nakakhuvula m'madzimo kasanunkaŵiri, malinga ndi m'mene adaamuuzira munthu wa Mulungu uja. Pompo adachira ndipo thupi lake lidangoti see ngati la kamwana, choncho adakhala woyeretsedwa. Pambuyo pake Naamani pamodzi ndi onse omperekeza, adabwerera kwa mneneri wa Mulungu uja. Adadzaima pamaso pa Elisa namuuza kuti, “Ndithu, ine ndadziŵa tsopano kuti pa dziko lonse lapansi kulibe Mulungu wina, koma wa ku Israele yekha. Tsono landirani mphatsoyi kwa ine mtumiki wanu.” Koma Elisa adati, “Pali Chauta, Mulungu wamoyo, amene ndimamtumikira, ine sindilandira zimenezi.” Naamani adamkakamiza kuti atenge, koma iye adakana ndithu. Tsono Naamani adati, “Ngati mukukana, ine ndikukupemphani kuti mundilole ine mtumiki wanu nditengeko dothi lokwanira kunyamula abulu aŵiri. Pakuti kuyambira tsopano ine sindidzaperekanso nsembe zopsereza, kapena nsembe ina iliyonse, kwa mulungu wina aliyense, koma kwa Chauta basi. Chauta andikhululukire ine pa chokhachi chakuti pamene mbuyanga mfumu akupita kukapembedza ku nyumba ya Chauta wake Rimoni, ine ndimatsagana naye ndipo ndimakagwada m'nyumba ya Rimoniyo. Chauta andikhululukire ine mtumiki wanu zimenezi.” Elisa adamuuza kuti, “Ai, inu kafikeni bwino.” Koma Naamani atangoyenda mtunda pang'ono, Gehazi, mtumiki wa Elisa mneneri wa Mulungu, adayamba kulingalira kuti, “Mbuyanga walekerera Naamani Msiriyayu, osalandira zimene adabwera nazo kudzapereka. Pali Chauta, Mulungu wamoyo, ine ndimthamangira kuti ndikalandireko kanthu.” Motero Gehazi adalondola Naamani uja. Naamani ataona kuti munthu akumthamangira, adatsika pa galeta kuti amchingamire. Tsono adafunsa kuti “Kodi nkwabwino?” Gehazi adati, “Inde, nkwabwino. Koma mbuyanga wandituma chifukwa tsopano apa kwangomufikira anthu aŵiri a m'gulu la aneneri, kuchokera ku dziko lamapiri la Efuremu. Tsono akukupemphani kuti chonde muŵapatseko ndalama zasiliva 3,000 ndi zovala ziŵiri zapaphwando.” Pamenepo Naamani adati, “Inu tengani ndithu ngakhale 6,000 zimene.” Choncho adamkakamiza, nalonga m'matumba ndalama za silivazo, pamodzi ndi zovala zapaphwandozo, nasenzetsa antchito ake aŵiri. Ndipo adanyamuka, antchitowo patsogolo, Gehazi pambuyo pao. Tsono Gehazi uja atafika kuphiri kumene kunali nyumba ya Elisa, adaŵalanda antchitowo ndalama zija nazilonga m'nyumba mwake. Ndipo adaŵauza kuti apite, iwo nkupita. Pambuyo pake Gehazi adapita kwa mbuyake. Elisa adamufunsa kuti, “Kodi Gehazi, unali kuti?” Iyeyo adati, “Sindidayende kwina kulikonse, bambo.” Koma Elisayo adamufunsanso kuti, “Kodi ukuyesa kuti sindidakuwone monse muja munthu uja amatsika pa galeta kuti adzakuchingamire? Kodi imeneyi inali nthaŵi yolandira ndalama ndi zovala, minda ya olivi ndi ya mphesa, kapena ng'ombe, akapolo kapena adzakazi? Ndiyetu tsono khate la Naamani lidzakumatirira iweyo ndi zidzukulu zako mpaka muyaya.” Motero Gehazi adatuluka m'nyumbamo ali ndi khate lambuu ngati chipale. Tsiku lina ena a m'gulu la aneneri adauza Elisa kuti, “Onani, malo tikukhala ndi inu ano akutichepera kwambiri. Mutilole tipite ku Yordani, tikadule nsichi imodzi-imodzi, kuti tidzakonze malo oti tizikhalamo.” Elisa adayankha kuti, “Chabwino, pitani.” Apo mmodzi mwa iwo adati, “Bwanji inuyo mupite nafe, atumiki anufe.” Elisa adavomera nati, “Tiyeni.” Choncho Elisayo adapita nawo. Atafika ku Yordani, anthu aja adayamba kudula mitengo. Koma pamene wina ankagwetsa nsichi, nkhwangwa yake idaguluka nigwa m'madzi, ndipo adafuula kuti, “Kalanga ine mbuyanga! Ndipotu nkhwangwa imeneyi njobwereka!” Tsono munthu wa Mulungu uja adafunsa kuti, “Kodi yagwera pati?” Atamuwonetsa malowo, Elisa adadula kamtengo nakaponya pamadzipo, nkhwangwayo nkuyandama. Ndipo Elisa adati, “Kaitole.” Munthu uja adatambalitsa dzanja, naigwira. Nthaŵi ina mfumu ya ku Siriya inkamenyana nkhondo ndi Aisraele. Ndipo idapangana ndi aphungu ake kuti, “Tikamange zithando zathu pa malo akutiakuti.” Koma mneneri Elisa adatumiza mau kwa mfumu ya ku Israele kuti, “Chenjerani ku malo akutiakutiŵa, poti Asiriya akukabisala kumeneko.” Tsono mfumu ya ku Israele idatuma anthu ku malo amene mneneri wa Mulungu uja adaanenaŵa. Umu ndimo m'mene mneneri ankachenjezera mfumu, kotero kuti idapulumuka kangapo konse. Tsono mfumu ya ku Siriya inkavutika kwambiri mu mtima chifukwa cha zimenezi. Choncho idaitana aphungu ake niŵafunsa kuti, “Kodi simungandiwuze pakati pathu pano munthu amene akuthandizira mfumu ya ku Israele?” Mmodzi mwa aphunguwo adayankha kuti, “Palibe ndi mmodzi yemwe, inu mbuyanga mfumu. Koma Elisa mneneri wa ku Israele ndiye amene amauza mfumu ya ku Israele mau amene inuyo mumalankhula kumbali m'chipinda mwanu.” Tsono mfumuyo idati, “Pitani mukaone kumene akukhala, kuti nditumeko anthu, akamgwire.” Anthuwo atabwerako, adamuuza kuti, “Ali ku Dotani.” Motero mfumuyo idatumako akavalo ndi magaleta, kudzanso gulu lalikulu la ankhondo. Ankhondowo adakafikako usiku, nazinga mzindawo. Tsono wantchito wa munthu wa Mulungu uja, atadzuka m'mamaŵa nkutuluka, adangoona gulu lankhondo lokwera pa akavalo ndi magaleta, litazinga mzinda wonsewo. Pomwepo wantchitoyo adabwerera nati, “Kalanga ine mbuyanga! Kodi titani?” Elisa adati, “Usachite mantha, pakuti amene ali pa mbali yathu ngambiri kupambana m'mene aliri iwoŵa.” Tsono Elisa adapemphera, adati, “Inu Chauta ndikukupemphani kuti mutsekule maso ake kuti apenye.” Motero Chauta adatsekula maso a wantchito uja, ndipo adangoona kuti phiri lili lodzaza ndi akavalo ndi magaleta amoto atamzungulira Elisa uja. Tsono pamene Asiriya adayamba kumthira nkhondo Elisa, iye adapemphera kwa Chauta, adati, “Ndikukupemphani kuti muŵachititse khungu anthu ameneŵa.” Motero Chauta adachititsa ankhondo aja khungu, monga momwe Elisa adapemphera. Ndipo Elisa adauza ankhondowo kuti, “Njira si imeneyi, ndipo mzinda si umenewunso ai. Tsatani ine, ndikakufikitsani kwa munthu amene mukumfunafunayo.” Choncho adaŵatsogolera mpaka ku Samariya. Atangoloŵa mu mzinda wa Samariyawo, Elisa uja adapemphera kuti, “Inu Chauta, atsekuleni maso anthuŵa apenye.” Choncho Chauta adatsekuladi maso ao, napenya. Ndipo adangoona kuti ali m'kati mwenimweni mwa Samariya. Tsono mfumu ya ku Israele itaona ankhondowo, idafunsa Elisa kuti, “Bambo wanga, kodi ndiŵaphe? Kodi ndiŵaphe?” Elisa adayankha kuti, “Usaŵaphe ai. Kodi ungaŵaphe anthu amene udachita kuŵagwira ukapolo pomenyana nawo nkhondo? Iyai, koma apatseni chakudya ndi madzi kuti ayambe apeza bwino, kenaka apite kwa mbuyao.” Motero adaŵakonzera madyerero aakulu. Atadya ndi kumwa, mfumuyo idaŵalola ankhondowo kuti achoke, ndipo iwo adapita kwa mbuyao. Pambuyo pake magulu ankhondo a Asiriya adaleka kuthira nkhondo dziko la Israele. Patapita nthaŵi ndithu, Benihadadi mfumu ya ku Siriya, adasonkhanitsa gulu lake lankhondo, napita kukazinga Samariya ndi zithando zankhondo. Ku Samariyako kunali njala yoopsa pa nthaŵi imene Asiriya ankazinga mzindawo ndi zithando zankhondo, mpaka kuti mutu wa bulu ankaugula ndi ndalama zasiliva 80. Ndipo magaramu 200 a zitosi za nkhunda ankagulitsa pamtengo wa masekeli asiliva asanu. Tsiku lina mfumu ikuyenda pa makoma a mzinda, mai wina adamfuulira kuti, “Inu mbuyanga mfumu, thandizeni.” Apo mfumuyo idafunsa kuti, “Kodi Chauta akapanda kukuthandiza, nanga ine ndingazipeze kuti zokuthandizira? Kodi kwatsalako kanthu ngati ku malo opunthira tirigu kapena ku malo opondera mphesa? Nanga chakuvuta nchiyani?” Iyeyo adayankha kuti, “Tsiku lina mai uyu adandiwuza kuti, ‘Ipha mwana wako kuti tidye lero, wanga tidye maŵa.’ Motero tidaphika mwana wangayo, ndipo tidadya. Tsono m'maŵa mwake ndidamuuza kuti, ‘Iphatu mwana wako uja kuti tidye.’ Koma iyeyu wabisa mwana wakeyo.” Mfumuyo itamva mau a maiwo idang'amba zovala zake. Pamenepo nkuti mfumuyo ikuyenda pa khoma. Ndipo anthu adangoona kuti mfumuyo yavala chiguduli m'kati mwa zovala zake. Tsono mfumu ija idati, “Mulungu andiphe, ndikapanda kudulitsa mutu wa Elisa mwana wa Safati lero.” Nthaŵiyo Elisa adaakhala pansi m'nyumba mwake, ndipo akuluakulu anali naye limodzi. Tsono mfumu ija idatuma mmodzi mwa atumiki ake kuti akatenge Elisa. Koma wamthengayo asanafike, Elisa adauza akuluakulu aja kuti, “Ha! Wopha anthu uja watuma munthu kuti adzandidule mutu. Akangofika wamthengayo, inu mutseke chitseko, ndipo muchigwiritse, asaloŵe. Kodi mgugu ukumveka pambuyo pakewo si wa mbuyake?” Elisayo akulankhulabe ndi akuluakuluwo, mfumu ija idafika, ndipo idati, “Mavuto ameneŵa watigwetsera ndi Chauta. Kodi ndingathe bwanji kudikira thandizo lochokera kwa Chauta?” Elisa adayankha nati, “Mverani, zimene akunena Chauta ndi izi, akuti, ‘Maŵa pa nthaŵi ngati yomwe ino makilogramu atatu a ufa wosalala adzaŵagulitsa pamtengo wa ndalama imodzi yasiliva, ndipo makilogramu asanu ndi limodzi a barele adzaŵagulitsanso pamtengo wa ndalama imodzi yasiliva ku chipata cha ku Samariya’ ” Tsono phungu wokhulupirika wa mfumu adafunsa munthu wa Mulungu uja kuti, “Ngakhale Chauta mwiniwake atachita kutikhuthulira mvula yochuluka chotani, zoterezi nkuchitika ngati?” Koma Elisa adati, “Ndithu udzaziwona zimenezo ndi maso ako, koma iweyo sudzazilaŵa.” Nthaŵi imeneyo panali anthu akhate anai amene ankakhala pa chipata. Iwowo adayamba kufunsana kuti, “Chifukwa chiyani tikungotambalala pano kumangodikira imfa? Tikati tiyeni tiloŵe mumzindamu, njala ili m'menemo kumene, ndiye tikaferamo. Komanso tikangotambalala pompano, tifabe. Tsono tiyeni tingopita ku zithando za Asiriya. Akatileka ndi moyo, chabwino, koma akatipha, palibe kanthu.” Motero adanyamuka ndi chisisira kupita ku zithando za Asiriya. Koma atafika ku malire a zithando za Asiriya, adaona kuti panalibe munthu ndi mmodzi yemwe. Chauta anali atamveketsa phokoso la magaleta ndi akavalo ndiponso mdidi wa gulu lankhondo pakati pa ankhondo a Asiriya. Ndiye iwowo adayamba kuuzana kuti, “Tamvani phokosolo, mfumu ya ku Israele yalemba mafumu a Ahiti ndi a Aejipito kuti adzatithire nkhondo!” Motero adathaŵa ndi chisisila, nasiya mahema, akavalo, abulu ndiponso katundu wao yense monga momwe adaaliri, nathaŵa kuti apulumutse moyo wao. Choncho akhate aja atafika ku malire a zithandozo, adakaloŵa mu hema limodzi, ndipo adadya ndi kumwa. Atatero adatengako siliva, golide ndi zovala, nakazibisa. Pambuyo pake adabwerera nakaloŵa mu hema linanso, natengamo zinthu, nkukazibisanso. Kenaka akhate aja adayamba kuuzana kuti, “Ife sitikuchita bwinotu pamenepa. Lero ndilo tsiku limene tili ndi uthenga wabwino kwambiri! Tikakhala chete ndi kumadikira mpaka m'maŵa, tidzalangidwa. Nchifukwa chake tsono tiyeni tikauze nduna za mfumu.” Motero adapita ku Samariya nakaitana alonda a pa chipata cha mzinda naŵauza kuti, “Ife tidaapita ku zithando za Asiriya, ndipo tidangoona kuti kulibe munthu ndi mmodzi yemwe. Ngakhale kumva mau sitidamve, koma tidangopeza akavalo okha pamodzi ndi abulu ali chimangire, ndiponso mahema monga momwe adaaliri.” Tsono alonda apachipata aja adalengeza uthengawo ndipo okhala kunyumba kwa mfumu adaumva. Pamenepo mfumu idadzuka usiku nikauza nduna zake kuti, “Ndikuuzeni zimene Asiriya atikonzera. Iwowo akudziŵa kuti ife tili ndi njala. Nchifukwa chake atuluka m'zithando kuti akabisale ku thengo. Choncho tikangotuluka mumzinda muno, iwowo atigwira amoyo ndipo aloŵa mumzinda muno.” Koma mmodzi mwa nduna zake adati, “Anthu a mumzinda muno posachedwa adzatsirizikanso monga Aisraele onse amene afa kaleŵa. Ndiye ife tiyeni tisankhe ena kuti atenge akavalo asanu amene atsalawo, tiŵatume kuti akaone.” Motero adasankha anthu aŵiri okwera pa akavalo, ndipo mfumuyo idaŵatuma kuti akalondole gulu la ankhondo la Asiriya. Idati, “Pitani mukaone chimene chachitika.” Anthu aja adaŵalondola Asiriya mpaka ku Yordani. Ndipo ndithu m'njira monse ankapeza zovala zili mbwee ndiponso katundu amene Asiriya ankapita nataya chifukwa cha kuthaŵa mofulumira. Pomwepo amithengawo adabwerera, nakauza mfumu. Tsono anthu a mu Samariya adatuluka nakafunkha ku zithando za Asiriya. Motero makilogramu atatu a ufa wosalala ankaŵagulitsadi pamtengo wa ndalama imodzi yasiliva, ndipo makilogramu asanu ndi limodzi a barele ankaŵagulitsanso chimodzimodzi potsata m'mene adaanenera Chauta. Pamene zinkachitika zimenezi, nkuti mfumu itaika phungu wake wokhulupirika uja kuti akhale wolamulira pa chipata. Koma anthu adapondereza phunguyo kuchipata kuja, kotero kuti adafa, monga momwe Elisa munthu wa Mulungu adaanenera pamene mfumu idaapita kukamuwona. Paja mneneri Elisa adaauza mfumu kuti, “Makilogramu asanu ndi limodzi a barele adzaŵagulitsa pamtengo wa ndalama imodzi yasiliva, ndipo makilogramu atatu a ufa wosalala adzaŵagulitsanso pamtengo wa ndalama imodzi yasiliva maŵa pa nthaŵi ngati yomwe ino ku chipata cha Samariya.” Pamenepo phungu wokhulupirika uja adaayankha Elisa munthu wa Mulungu uja, kuti, “Ngakhale Chauta mwiniwake atachita kutikhuthulira mvula yochuluka chotani, zoterezi nkuchitika ngati?” Apo mpamene Elisa adaamuuza kuti, “Ndithu udzaziwona zimenezo ndi maso ako, koma iweyo sudzazilaŵa.” Motero zidamchitikiradi, pakuti anthu adampondereza pa chipata ndipo adafera pomwepo. Ndiye kuti Elisa anali atauza mai amene adaamuukitsira mwana wake uja kuti, “Nyamuka upite pamodzi ndi a pabanja pako, ukakhale nawo kulikonse kumene ungathe kukakhala, pakuti Chauta akubweretsa pa dziko njala ya zaka zisanu ndi ziŵiri.” Motero maiyo adanyamuka, ndipo adachitadi monga momwe munthu wa Mulungu uja adaanenera. Adapita pamodzi ndi a pabanja pake, nakakhala nawo ku dziko la Afilisti zaka zisanu ndi ziŵiri. Tsono zitatha zaka zisanu ndi ziŵirizo, mai uja adabwerako ku dziko la Afilisti kuja, ndipo adapitanso kwa mfumu ya ku Israele kukafunsa za nyumba yake ndi munda wake. Atafika kwa mfumu, adapeza mfumuyo ikulankhula ndi Gehazi, mtumiki wa munthu wa Mulungu uja, nimafunsa kuti, “Tandiwuza zonse zikuluzikulu zimene Elisa wachita.” Pamene mtumikiyo ankauza mfumuyo m'mene Elisa adaukitsira anthu akufa, mkazi uja, amene mwana wake Elisa adamuukitsira, adadzafunsa mfumu za nyumba yake ndi munda wake. Pamenepo Gehazi adati, “Inu mbuyanga mfumu, pano pali mai, ndipo mwana wake ndi uyu amene Elisa adamuukitsa.” Mfumu itamufunsa maiyo, iyeyo adaifotokozera kuti Elisa adaukitsadi mwana wake. Choncho mfumu ija idamuikira nduna maiyo niiwuza kuti, “Umbwezere zonse zimene zidaali zake, pamodzi ndi phindu lonse lochokera ku zokolola za kumunda kwake, kuyambira tsiku limene adachoka mpaka tsopano lino.” Tsiku lina Elisa adapita ku Damasiko, pa nthaŵi imene Benihadadi mfumu ya ku Siriya ankadwala. Mfumuyo itamva kuti kwabwera munthu wa Mulungu, idauza Hazaele nduna yake yaikulu kuti, “Tenga mphatso, upite kukakumana naye munthu wa Mulunguyo. Tsono upemphe nzeru kwa Chauta kudzera mwa iyeyo kuti, ‘Kodi mfumu idzachira matenda ameneŵa?’ ” Motero Hazaele adapita kukakumana ndi mneneri Elisa, atasenzetsa ngamira 40 mphatso ndi zinthu zokoma zosiyanasiyana za ku Damasiko. Atafika, adakaima pamaso pa Elisa, munthu wa Mulungu uja, nati, “Munthu wanu Benihadadi, mfumu ya ku Siriya, wandituma kuti ndikufunseni kuti, kodi ati adzachira?” Elisa adayankha kuti, “Chauta wandiwonetsa kuti adzafa, komabe pita ukamuuze kuti adzachira.” Atatero, Elisa adamuyang'ana kwambiri Hazaele mpaka adachita manyazi. Apo Elisayo adayamba kulira. Tsono Hazaele adamufunsa kuti, “Mbuyanga, mukuliranji?” Iyeyo adayankha kuti, “Chifukwa ndikudziŵa zoipa zimene mudzaŵachita Aisraele. Mudzatentha malinga ao ankhondo ndipo mudzapha ankhondo ao ambiri. Mudzapondereza tiana tao, ndipo mudzang'amba akazi ao apakati.” Apo Hazaele adafunsa kuti, “Kodi kapolo wanune amene ndine wonyozeka ngati galu, ndingathe bwanji kuchita zinthu zazikulu zoterezi?” Elisa adayankha kuti, “Chauta wandiwonetsa kuti iweyo udzakhala mfumu ya Asiriya.” Pomwepo Hazaeleyo adasiyana naye Elisa, napita kwa mbuyake. Mbuyakeyo adamufunsa kuti, “Kodi Elisa wakuuza zotani?” Hazaele adayankha kuti, “Inuyo muchira ndithu.” Koma m'maŵa mwake, Hazaele adatenga chofunda nachiviika m'madzi nkuchiphimba kumaso kwa mfumu, ndipo mfumu ija idafa. Motero Hazaele adaloŵa ufumu m'malo mwake. Chaka chachisanu cha ufumu wa Yoramu, mwana wa Ahabu mfumu ya ku Israele, Yehoramu, mwana wa Yehosafati mfumu ya ku Yuda, adayambapo kulamulira dziko la Yuda. Yehoramu anali ndi zaka 32 pamene ankaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka zisanu ndi zitatu ku Yerusalemu. Tsono Yehoramuyo ankatsata makhalidwe oipa a mafumu a ku Aisraele, monga m'mene linkachitira banja la Ahabu, pakuti adaakwatira mwana wa Ahabu. Tsono ankachita zoipa zili zonse pamaso pa Chauta. Komabe Chauta sadafune kuwononga Yuda, chifukwa cha Davide mtumiki wake, popeza kuti Chauta adaalonjeza kuti adzampatsa nyale Davide ndi zidzukulu zake mpaka muyaya. Pa nthaŵi yakeyo anthu a ku Edomu adaukira ulamuliro wa Yuda ndipo adadzisankhira mfumu yao. Tsono Yehoramu adapita ku Zairi pamodzi ndi magaleta ake onse ankhondo. Adanyamuka usiku nakaŵakantha Aedomu amene adaamzinga iyeyo pamodzi ndi atsogoleri a magaleta ake. Ankhondo ake onse adathawa napita kwao. Motero Aedomu ngoukira ulamuliro wa Yuda mpaka lero lino. Pa nthaŵi imeneyo mzinda wa Libina nawonso udaukira ulamuliro wake. Tsono ntchito zina za Yehoramu, ndi zonse zimene adazichita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda. Choncho Yehoramu adamwalira naikidwa m'manda momwe adaikidwa makolo akewo mu mzinda wa Davide. Ndipo Ahaziya mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Pa chaka cha 12 cha ufumu wa Yoramu, mwana wa Ahabu, mfumu ya ku Israele, Ahaziya mwana wa Yehoramu, mfumu ya ku Yuda, adayamba kulamulira. Ahaziya anali ndi zaka 22 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira chaka chimodzi ku Yerusalemu. Mai wake anali Ataliya, mdzukulu wake wa Omuri mfumu ya ku Israele. Iyeyonso ankatsata chitsanzo choipa cha banja la Ahabu. Adachita zoipa pamaso pa Chauta monga m'mene linkachitira banja la Ahabu, poti anali mkamwini m'banja la Ahabu lomwelo. Tsono mfumu Ahaziya adapita pamodzi ndi Yoramu, mwana wa Ahabu, kuti akamenyane nkhondo ndi Hazaele, mfumu ya ku Siriya, ku Ramoti ku Giliyadi. Kumeneko Asiriya adalasa Yoramu. Tsono Yoramuyo adabwerera napita ku Yezireele, kuti akamchiritse mabala amene Asiriya adaamlasa ku Rama, pamene ankamenyana ndi Hazaele mfumu ya ku Siriya. Motero Ahaziya, mwana wa Yehoramu, mfumu ya ku Yuda, adapita ku Yezireele kukazonda Yoramu mwana wa Ahabu, chifukwa chakuti ankadwala. Masiku amenewo Elisa adaitana mmodzi wa m'gulu la aneneri, namuuza kuti, “Konzekera ulendo ndipo utenge nsupa iyi ya mafuta m'manja, upite ku Ramoti-Giliyadi. Ukakafika, ukafunefune Yehu, mwana wa Yehosafati, mdzukulu wa Nimisi. Utampeza ukamuuze kuti achokepo pakati pa anzake, ndipo ukaloŵe naye m'chipinda cham'kati. Tsono ukathire mafutaŵa pamutu pake, ndipo ukanene kuti, ‘Chauta akukudzoza kuti ukhale mfumu ya ku Israele.’ Pomwepo ukatsekule chitseko ndipo ukathaŵe, usakachedwe ai.” Motero mneneriyo adapita ku Ramoti-Giliyadi. Atafika, adapeza atsogoleri ankhondo ali pa msonkhano. Tsono iyeyo adati, “Zikomo bwana, ine ndili ndi mau oti ndikuuzeni.” Yehu adafunsa kuti, “Kodi ukunena yani mwa ifeyo?” Mneneri uja adayankha nati, “Inuyo bwana.” Pamenepo Yehuyo adanyamuka nakaloŵa m'nyumba. Ndipo mneneri uja adathira mafuta pamutu pa Yehu nati, “Chauta, Mulungu wa Israele, akuti akukudzozani inu kuti mukhale mfumu ya Aisraele, anthu a Chauta. Tsono mukakanthe banja la Ahabu mbuyanu, kuti Chautayo alipsire Yezebele, chifukwa cha aneneri ake ndiponso atumiki ena onse amene iyeyo adaŵapha. Ndithu banja lonse la Ahabu lidzatha phu! Ku Israele adzapha mwamuna aliyense wa banja la Ahabu, kapolo kapena mfulu. Tsono Chautayo adzasandutsa banja la Ahabu kuti lifanane ndi banja la Yerobowamu mwana wa Nebati, ndiponso la Baasa mwana wa Ahiya. Ndipo agalu adzamudya Yezebele ku dziko la Yezireele. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzamuike.” Atanena mau amenewo, mneneri uja adatsekula chitseko, nathaŵa. Tsono Yehu atatuluka kubwerera kwa atsogoleri anzake aja, iwo adamufunsa kuti, “Kodi nkwabwino? Wamsala uja anadzatani kwa inu?” Yehu adayankha kuti “Ai, mukumdziŵa munthu wotere ndi zolankhula zake zomwe.” Koma iwowo adati, “Iyai ndithu, mutiwuze.” Apo Yehu adati, “Iyeyo wandiwuza mau a Chauta akuti, ‘Ine ndikukudzoza iwe kuti ukhale mfumu ya ku Israele.’ ” Pomwepo aliyense mwa iwowo adatenga mwinjiro wake nauyala pa makwerero, kuti Yehu akhalepo, ndipo adaliza lipenga, nalengeza kuti, “Yehu ndiye mfumu.” Motero Yehu, mwana wa Yehosafati, mdzukulu wa Nimisi, adachita chiwembu mfumu Yoramu. Pomwe zinkachitika zimenezi, nkuti Yoramu pamodzi ndi Aisraele onse akudikira Hazaele mfumu ya Asiriya ku Ramoti-Giliyadi, kuti amenyane naye nkhondo. Koma nthaŵiyo mfumu Yoramu anali atabwerera ku Yezireele, kuti akachire mabala amene adamlasa Asiriya aja pa nthaŵi imene ankamenyana nkhondo ndi Hazaele uja. Tsono Yehu adauza atsogoleri ankhondo anzake aja kuti, “Ngati mufuna kuti ndikhale mfumu, musalole ndi mmodzi yemwe kuti achoke mumzinda muno, kuti akanene nkhani zimenezi ku Yezireele.” Apo Yehu adakwera galeta lake, napita ku Yezireele poti Yoramu anali chigonere kumeneko. Ahaziya, mfumu ya ku Yuda, anali atabwera komweko kudzacheza ndi Yoramuyo. Tsono mlonda amene ankaimirira pa nsanja yolondera mzinda wa Yezireele, adaona gulu lankhondo la Yehu likubwera, ndipo adati, “Ndikuwona gulu lankhondo.” Pompo Yoramu adati, “Tuma munthu pa kavalo kuti akumane nawo, ndipo akafunse kuti, ‘Kodi ndi zamtendere?’ ” Munthu wokwera pa kavalo uja adapita kukakumana nawo nati, “Mfumu ikufunsa kuti, ‘Kodi ndi zamtendere?’ ” Yehu adayankha kuti, “Kodi iweyo nkhani ya mtendere uli nayo chiyani? Tiye, uzinditsata pambuyo.” Mlonda uja adakanena kwa mfumu Yoramu kuti, “Wamthenga uja wakafika ndithu kwa anthuwo, koma sakubwerako ai.” Tsono Yoramu adatumanso munthu wachiŵiri wokwera pa kavalo, amene adakafika kwa anthuwo nakaŵafunsanso kuti, “Mfumu ikufunsa kuti, ‘Kodi ndi zamtendere?’ ” Apo Yehu adayankhanso kuti, “Kodi iweyo nkhani ya mtendere uli nayo chiyani? Tiye, uzinditsata pambuyo.” Mlonda uja adakanenanso kuti, “Amene ujanso wakafika kwa anthuwo, koma sakubwerako ai. Ndipo kuthamanga kwa mtsogoleri wa gululo nkoopsa, ndi ngati m'mene amathamangira Yehu mwana wa Nimisi.” Atamva zimenezo Yoramu adati, “Konzekani.” Pomwepo anthuwo adakonza galeta lake. Tsono Yoramu mfumu ya ku Israele, pamodzi ndi Ahaziya mfumu ya ku Yuda, adanyamuka, wina m'galeta mwake, winanso mwake, ndipo adakumana ndi Yehu pa munda wa Naboti wa ku Yezireele uja. Yoramu ataona Yehu, adafunsa kuti, “Iwe Yehu, kodi ndi zamtendere?” Iyeyo adayankha kuti, “Kodi pangakhale mtendere bwanji pamene za kupembedza mafano ndi zanyanga zimene adayamba mai wako zikupitirirabe?” Apo Yoramu adabwevuka nathaŵa, ndipo adafuulira Ahaziya uja kuti, “Iwe Ahaziya, atiwukira anthuŵa.” Tsono Yehu adakoka uta ndi mphamvu zake zonse nalasa Yoramu kumsana pakati pa mapewa, kotero kuti muvi udaloŵa mpaka ku mtima, ndipo adagwera m'galeta momwemo. Pompo Yehu adauza Bidikari kapitao wake kuti, “Mnyamule, umponye m'munda wa Naboti wa ku Yezireele. Kumbukira kuti muja ine ndi iwe tinkayenda pambuyo pa Ahabu atate ake a Yoramu, Chauta adaamtemberera kuti, ‘Ndithudi monga m'mene ndidaonera kuphedwa kwa Naboti ndi ana ake dzulo, ndikukuuza kuti Ine ndidzakubwezera choipa chimenechi pamunda pompano.’ Nchifukwa chake tsono, mtengeni, mumponye m'mundamu, potsata zimene Chauta adaanena.” Tsono Ahaziya mfumu ya ku Yuda ataona zimenezi, adathaŵira ku Betehagani. Koma Yehu adamlondola nati, “Nayenso mlaseni.” Ndipo adamlasira m'galeta pa chitunda cha Guri, pafupi ndi Ibleamu. Tsono Ahaziya adathaŵira ku Megido, nakafera komweko. Nduna zake zidamnyamulira m'galeta kunka naye ku Yerusalemu, ndipo zidamuika m'manda momwe adaikidwa makolo ake mu mzinda wa Davide. Pa chaka cha 11 cha ufumu wa Yoramu mwana wa Ahabu, mpamene Ahaziya adaayamba kulamulira Yuda. Yehu atafika ku Yezireele, Yezibele adamva zimene zidachitika. Ndipo adapaka maso ake utoto, naluka tsitsi lake, namasuzumira pa windo. Tsono pamene Yehu ankaloŵa pa chipata, Yezibeleyo adamkuwira nati, “Inu aZimuri, amene mudapha mbuyanu, kodi ndi zamtendere?” Yehu adayang'ana ku zenera nati, “Kodi akugwirizana ndi ine ndani?” Tsono atumiki aŵiri kapena atatu a ku bwalo la mfumu adayang'ana Yehu uja. Iyeyo adaŵalamula kuti, “Mponyeni pansi mkaziyo.” Pomwepo iwo adamponya pansi, ndipo magazi ake ena adafalikira pa khoma ndi pa akavalo. Kenaka Yehu adayendetsa akavalo ake nkumpondereza mkaziyo. Pambuyo pake Yehu adaloŵa m'nyumba yaufumu naadya ndi kumwa. Kenaka adati, “Kamtoleni mkazi wotembereredwa uja, mukamuike, pakuti ndi mwana wa mfumu.” Koma pamene ankapita kuti akamuike, sadapezepo nkanthu komwe koma chibade, mapazi ndi zikhatho za manja ake basi. Atabwererako anthuwo ndi kukamuuza Yehu, iyeyo adati, “Ameneŵa ndiwo mau a Chauta amene adalankhula kudzera mwa Eliya mtumiki wake wa ku Tisibe, kuti, ‘Agalu adzadya mtembo wa Yezibele ku dziko la Yezireele. Motero mtembo wakewo udzakhala ngati ndoŵe pa munda m'dziko la Yezireele, kotero kuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzatha kunena kuti, “Uyu ndi Yezibele.” ’ ” Mfumu Ahabu anali ndi zidzukulu zazimuna 70 ku Samariya. Tsono Yehu adalemba makalata naŵatumiza ku Samariya kwa olamulira mzindawo, kwa akuluakulu ndiponso kwa anthu amene ankalera zidzukulu za Ahabu kuti, “Inu mukusamalira zidzukulu za mbuyanu Ahabu, ndipo muli nawo magaleta, zida zankhondo ndiponso mizinda yamalinga. Nchifukwa chake tsono mukangolandira kalatayi, mwa zidzukulu za mbuyanu musankhule mmodzi wooneka bwino kwambiri ndipo mumloŵetse ufumu wa bambo wake. Kenaka mukonzekere nkhondo kumenyera banja la mbuyanu.” Koma anthuwo adachita mantha kwambiri, ndipo adati, “Ha! Mafumu aŵiri aja sadathe kulimbana naye Yehu, nanga ife ndiye tingathe bwanji?” Motero woyang'anira nyumba ya mfumu ndiponso wina woyang'anira mzinda, pamodzi ndi akuluakulu, kudzanso amene ankalera anawo, adatumiza mau kwa Yehu kuti, “Ife ndife anthu anu, ndipo tidzachita zonse zimene mutiwuze. Sitidzaika wina aliyense kuti akhale mfumu. Muchite zonse zimene zikukomereni.” Tsono Yehu adaŵalemberanso kalata yachiŵiri kuti, “Ngati muli pambuyo panga, ndipo ngati muli okonzeka kundimvera, mudule mitu ya ana a mbuyanu, mudze nayo kwa ine ku Yezireele maŵa nthaŵi yonga yomwe ino.” Ndiye kuti zidzukulu za mfumu 70 zija zinkaleredwa ndi akuluakulu amumzinda aja. Ndiye akuluakuluwo atalandira kalata ija, adagwira zidzukulu za mfumuzo nkuzipha, 70 zonsezo, naika mitu yao m'madengu, nkuitumiza kwa Yehu ku Yezireele. Tsono wamthenga adafika nauza Yehu kuti, “Abwera nayo mitu ija ya zidzukulu za mfumuyi.” Apo iyeyo adati, “Kaiwunjikeni m'miyulu iŵiri pa chipata, ndipo ikhale pamenepo mpaka m'maŵa.” M'maŵa mwake atatuluka, Yehu adapitako nauza anthu onse kuti, “Inu sindinu ochimwa ai. Wochimwa ndine, popeza kuti ndidachita chiwembu mbuyanga, ndipo ndidamupha. Koma adapha anthu onseŵa ndani? Dziŵani tsono kuti mau a Chauta, amene adanena za banja la Ahabu, sadzapita padera. Ndi Chauta amene wachitadi zimene adalankhula kudzera mwa Eliya mtumiki wake.” Pambuyo pake Yehu adapha onse otsala a banja la Ahabu ku Yezireele, akuluakulu ake onse, abwenzi ake onse ozoloŵerana naye ndiponso ansembe ake. Sadasiyepo ndi mmodzi yemwe. Pambuyo pake Yehu adanyamuka napita ku Samariya. Atafika pa malo otchedwa “Pogona abusa,” adakumana ndi abale ake a Ahaziya mfumu ya Yuda. Adaŵafunsa kuti, “Nanga inunso ndinu yani?” Iwo adayankha kuti, “Ndife abale a malemu Ahaziya, ndipo tidabwera kudzacheza ndi ana a mfumu Ahabu, ndiponso ana a mfumukazi Yezebele.” Tsono Yehu adati, “Atengeni amoyo.” Ndipo adaŵatenga amoyo, nakaŵaphera ku chitsime cha ku malo aja a abusaŵa, anthu okwanira 42. Sadasiyepo ndi mmodzi yemwe. Atachoka kumeneko, Yehu adakumana ndi Yehonadabu mwana wa Rekabu akudzamchingamira. Tsono adamlonjera namuuza kuti, “Kodi maganizo ako akugwirizana ndi maganizo anga, monga momwe maganizo anga akugwirizanirana ndi ako?” Yehonadabu adayankha kuti, “Inde, zathu nzimodzi.” Yehu adati, “Ngati ndi momwemodi, gwire dzanja.” Yehonadabuyo adapereka dzanja lake, Yehu nkumgwira dzanja namkweza pa galeta lake. Ndipo adamuuza kuti, “Tiye kuno, uwone m'mene ndikudziperekera kwa Chauta.” Motero adayenda naye m'galeta mwake. Atafika ku Samariya, Yehu adapha onse amene adatsalako a banja la Ahabu, mpaka adaŵapulula onse, potsata mau a Chauta amene Eliya adaŵalankhula. Pambuyo pake Yehu adasonkhanitsa anthu onse a mu mzinda wa Samariya naŵauza kuti, “Ahabu ankatumikira Baala pang'ono chabe. Koma ine Yehu ndidzamtumikira kwambiri. Nchifukwa chake tsono itanireni aneneri onse a Baala, onse amene amapembedza Baalayo, pamodzi ndi ansembe ake onse. Pasasoŵeke ndi mmodzi yemwe, poti ndili ndi nsembe yaikulu yoti ndiipereke kwa Baala. Amene asoŵeke, adzaphedwa.” Koma Yehu adachita zimenezi mochenjera, kuti aononge onse amene ankapembedza Baala. Motero Yehu adalamula kuti: “Mulengeze kuti kuli msonkhano wolemekeza Baala.” Anthu adaulengezadi msonkhanowo. Yehu adatumiza mau ku dziko lonse la Israele, ndipo onse amene ankapembedza Baala adabweradi, kotero kuti sadatsalepo ndi mmodzi yemwe. Onsewo adaloŵa m'nyumba ya Baala, ndipo anthu adachita kuti thothotho m'nyumbamo. Sipadatsale malo mpang'ono pomwe. Tsono Yehu adauza munthu wosunga zovala kuti, “Bwera ndi zovala zopatulika zokwanira anthu onse opembedza Baala.” Munthuyo adaŵatengera zovalazo anthu aja. Yehu adaloŵa m'nyumba ya Baala pamodzi ndi Yehonadabu mwana wa Rekabu. Ndipo adauza anthu aja opembedza Baalaŵa kuti: “Yang'anani bwino, ndipo muwone kuti pasakhale mtumiki wa Chauta pano pakati panupa, koma opembedza Baala okhaokha.” Tsono Yehu adaloŵa kukapereka nsembe zopsereza. Koma Yehu anali ataika anthu 80 panja naŵauza kuti, “Adzaphedwa amene athaŵitse aliyense mwa anthu amene ndikupatseni kuti muŵapheŵa.” Tsono Yehu uja atangomaliza kupereka nsembe yopsereza ija, adauza asilikali ake ndi akapitao ao kuti: “Loŵani muŵaphe! Asapulumukepo ndi mmodzi yemwe.” Iwo adaloŵadi, nkukapha onse amene anali m'menemo, naponya mitembo yao panja. Adakaloŵanso m'chipinda cham'kati cha nyumba ya Baala ija. Ndipo adatulutsamo chipilala chopatulika chimene chinali m'nyumba ya Baala nakachitentha. Motero asilikaliwo adaononga chipilala chopatulika cha Baala, naononganso nyumba yake, ndipo adaisandutsa chimbudzi mpaka lero lino. Motero Yehu adaononga kotheratu chipembedzo cha Baala m'dziko la Israele. Koma Yehuyo sadaleke kwenikweni zoipa zimene ankachita mfumu Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene ankachimwitsa nazo Aisraele. Sadaleke kupembedza zifanizo zagolide za anaang'ombe zimene zinali ku Betele ndi ku Dani. Ndipo Chauta adauza Yehu kuti: “Chifukwa choti wachita zondikomera Ine, poononga banja la Ahabu monga momwe ndinkafunira, ana ako adzakhala pa mpando waufumu wa Israele mpaka mbadwo wachinai.” Koma Yehuyo sankasamala Malamulo a Chauta, Mulungu wa Israele, ndi mtima wake wonse. Adapitirizabe kuchita zoipa zimene Yerobowamu adachimwitsa nazo Aisraele. Masiku amenewo Chauta adayamba kuchepetsa dziko la Israele. Mfumu Hazaele wa ku Siriya adagonjetsa Aisraele. Adayambira ku Yordani chakuvuma, nakafika ku Aroere pafupi ndi chigwa cha Arinoni. Dziko limeneli lidaphatikiza madera onse a Giliyadi ndi Basani, kumene zinkakhala zidzukulu za Gadi, Rubeni ndi Manase. Tsono ntchito zina za Yehu ndi zonse zimene adazichita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele. Yehu adamwalira, naikidwa m'manda mu mzinda wa Samariya. Ndipo Yohowahazi mwana wake adaloŵa ufumu ku Israele m'malo mwake. Yehu adalamulira Aisraele ku Samariya zaka 28. Ataliya, mai wake wa Ahaziya, ataona kuti mwana wake wafa, adanyamuka nakaononga onse a pa banja laufumu. Koma Yehoseba, mwana wamkazi wa mfumu Yehoramu, mlongo wake wa Ahaziya, adatenga Yowasi, mwana wa Ahaziya. Adachita momuba, kumchotsa pakati pa ana aamuna a mfumu amene ankati aŵaphewo. Adamuika m'chipinda china chogona cha m'Nyumba ya Chauta pamodzi ndi mlezi wake. Motero adamubisa mwanayo, kubisira Ataliya, kotero kuti sadaphedwe. Mwanayo adakhala ndi mlezi wake zaka zisanu ndi chimodzi akubisala m'Nyumba ya Chauta, pamene Ataliya ankalamulira dzikolo. Koma chaka chachisanu ndi chiŵiri, wansembe Yehoyada adatumiza mau kukaitana atsogoleri a asilikali olonda mfumu ndipo a alonda a nyumba yaufumu. Adabwera nawo kwa Yehoyada ku Nyumba ya Chauta. Tsono adapangana nawo chipangano ndipo adaŵalumbiritsa m'Nyumba ya Chauta. Kenaka adaŵaonetsa mwana wamwamuna wa mfumu uja, naŵalamula kuti, “Zimene mudzachite ndi izi: Inu a m'chigaŵo chija choyamba, amene mukudzatumikira pa Sabata, mugaŵikane patatu: gulu limodzi lidzalonde ku nyumba ya mfumu; gulu lachiŵiri lidzalonde pa Chipata cha Suri, gulu lachitatu lidzalonde pa chipata cha kumbuyo kwa asilikali, azilonda pa zipata zoloŵera ku Nyumba ya Chauta. Tsono enawo a m'zigawo ziŵiri zija odzaŵeruka ntchito pa Sabata, iwo adzalonde ku Nyumba ya Chauta, kuti aziteteza mfumu. Mudzazungulire mfumuyo, aliyense atatenga zida m'manja. Wina aliyense amene at ayandikire pafupi, aphedwe. Muzikhala nayo mfumu kulikonse kumene iziyenda.” Atsogoleriwo adachitadi zonse monga m'mene wansembe Yehoyada adaŵalamulira. Aliyense adabwera ndi anthu ake amene ankadzayamba ntchito yao pa Sabata, pamodzinso ndi anthu amene ankasiya ntchito yao kulonda pa Sabata. Onsewo adafika kwa Yehoyada wansembe uja. Wansembeyo adapatsa atsogoleri aja mikondo ndi zishango, zimene zidaali za mfumu Davide. Zimenezi zinkasungidwa m'Nyumba ya Chauta. Tsono adandanditsa asilikaliwo kuti aziteteza mfumu, aliyense ali ndi zida m'manja mwake, kuzungulira guwalo ndiponso Nyumbayo. Kenaka adaŵatulutsira mwana wa mfumu, namuveka chisoti chaufumu, nkumupatsa buku la malamulo, ndipo adamdzoza namlonga ufumu. Anthu adamuwombera m'manja nkunena mofuula kuti, “Amfumu akhale ndi moyo wautali.” Tsono mfumukazi Ataliya, atamva phokoso la asilikali ndi la anthu, adapita ku Nyumba ya Chauta. Atayang'ana, adaona mfumu itaima pa nsanja yake potsata mwambo wachifumu, atsogoleri ndi anthu oimba malipenga ali pafupi ndi mfumuyo. Anthu onse am'deralo ankakondwa, namaimba malipenga. Pamenepo Ataliyayo adang'amba zovala zake, ndipo mofuula adati, “Akundiwukira! Akundiwukira!” Tsono wansembe Yehoyada adalamula atsogoleri a gulu lankhondo aja kuti, “Mtulutseni ameneyu pakati pa mizere mwandandayo. Ndipo aliyense amene amtsate, mumuphe ndi lupanga.” Wansembeyo adaanenadi kuti, “Musamphere m'Nyumba ya Chauta ai.” Choncho anthuwo adamgwira Ataliya uja, ndipo atafika naye ku nyumba ya mfumu, pakhomo lotchedwa la Akavalo, adamuphera pamenepo. Tsono Yehoyada adachititsa chipangano pakati pa Chauta ndi mfumu pamodzi ndi anthu ake, kuti iwowo akhale anthu akeake a Chauta. Anthuwo adachitanso chipangano ndi mfumu, Choncho anthu onse a m'dzikomo adapita ku nyumba ya Baala nakaigwetsa. Maguwa ake ndi mafano ake adaŵaphwanyaphwanya. Kenako adapha Matani wansembe wa Baala patsogolo pa maguwa pomwepo. Tsono wansembe Yehoyada adaika alonda ku Nyumba ya Chauta. Pambuyo pake iyeyo adandanditsa atsogoleri a ankhondo, asilikali olonda mfumu, alonda a nyumba ya mfumu, ndi anthu onse a m'dzikomo. Onsewo adaperekeza mfumu kuchokera ku Nyumba ya Chauta, nadzera ku chipata cha alonda mpaka kukafika ku nyumba ya mfumu. Pomwepo Yowasi adakhala pa mpando waufumu. Motero anthu am'dzikomo adakondwa. Ndipo mumzindamo mudakhala bata, Ataliya ataphedwa ku nyumba ya mfumu. Yowasiyo anali wa zaka zisanu ndi ziŵiri pamene adaloŵa ufumu. Chaka chachisanu ndi chiŵiri cha ufumu wa Yehu, Yowasi adaloŵa ufumu ndipo adalamulira zaka makumi anai ku Yerusalemu. Mai wake anali Zibiya wa ku Beereseba. Tsono Yowasiyo adachita zolungama pamaso pa Chauta masiku onse a moyo wake, chifukwa choti Yehoyada, wansembe uja, ankamlangiza. Komabe akachisi opembedzerako mafano pa zitunda sadaŵaononge. Anthu adapitirirabe kupereka nsembe ndi kumafukiza lubani pa malo amenewo. Nthaŵi ina mfumu Yowasi adauza ansembe kuti, “Musunge bwino ndalama zonse zimene zimaperekedwa ngati zopereka zopatulika ku Nyumba ya Chauta, ndiye kuti ndalama za msonkho wa munthu aliyense, ndiponso ndalama zimene munthu amapereka mwaufulu ku Nyumba ya Chauta. Wansembe aliyense aziyang'anira ndalama zopereka anthu amene iye amaŵatumikira, ndipo azigwiritse ntchito pokonza Nyumba paliponse pamene pafunika kukonza.” Koma pomafika chaka cha 23 cha ufumu wa Yowasi, ansembewo anali asanakonzebe Nyumbayo. Nchifukwa chake mfumu Yowasi adaitana wansembe Yehoyada ndi ansembe ena, naŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani simukukonza Nyumbayi? Kuyambira tsopano, musasungenso ndalama za anthu amene mumaŵatumikira, koma muzipereke kuti akonzere Nyumbayi.” Motero ansembe aja adavomera kuti sadzatenganso ndalama kwa anthu, ndipo kuti sindiwo adzakonza Nyumbayo, koma ena. Tsono wansembe Yehoyada adatenga bokosi, ndipo adaboola chivundikiro chake, naika bokosilo pambali pa guwa cha ku dzanja lamanja kwa aliyense woloŵa m'Nyumba ya Chauta. Ansembe amene anali pa khomo ankaponyamo ndalama zonse zimene anthu ankabwera nazo ku Nyumba ya Chauta. Nthaŵi zonse ankati akaona kuti m'bokosimo muli ndalama zambiri, mlembi wa mfumu ndi mkulu wa ansembe ankabwera kudzaŵerenga ndi kumanga m'matumba ndalama zimene zinali m'Nyumba ya Chauta. Tsono ndalamazo ataziyesa, ankazipereka kwa akapitao okonzetsa Nyumba ya Chauta aja. Iwowo ankalipira amisiri a matabwa ndi amisiri omanga nyumba, amene ankagwira ntchito yokonza Nyumba ya Chautayo. Ankalipiranso amisiri omanga ndi miyala ndi osema miyala, ndiponso ankagula mitengo ndi miyala yokumba yokonzera Nyumba ya Chauta, kudzanso zinthu zina zilizonse zofunikira poikonza. Koma mabeseni asiliva a ku Nyumba ya Chauta, ngakhale mbano, mbale, malipenga, ziŵiya zagolide ndi zasiliva, sadagule ndi ndalama zimene zinkabwera ku Nyumba ya Chauta, pakuti zimenezo ankalipirira antchito okonza Nyumba ya Chauta. Anthu amene ankaŵapatsa ndalama zolipirira antchito okonza Nyumbawo, sankaŵafunsa kuti afotokoze za kamwazidwe ka ndalamazo, popeza kuti anali anthu okhulupirika. Ndalama zoperekera nsembe zolipira mlandu ndiponso ndalama zoperekera nsembe zopepesera machimo, sankaziponya m'bokosi la m'Nyumba ya Chauta. Zimenezo zinali za ansembe. Nthaŵi imeneyo Hazaele, mfumu ya ku Siriya, adathira nkhondo mzinda wa Gati, ndipo adaulanda mzindawo. Kenaka Hazaele adatsimikiza mtima kuti akathire nkhondo ku Yerusalemu. Koma Yowasi mfumu ya ku Yuda adatenga zopereka zonse zopatulika zimene Yehosafati, Yehoramu ndi Ahaziya, makolo ake, mafumu a ku Yuda, adazipereka kwa Mulungu pamodzi ndi mphatso zakezake zopatulika, kudzanso golide yense amene adampeza m'nyumba zosungira chuma cha ku Nyumba ya Chauta ndi cha ku nyumba ya mfumu. Zonsezo adazitumiza ngati mphatso zopepesera Hazaele mfumu ya ku Siriya. Tsono Hazaele adazilandira nachokako ku Yerusalemu. Tsono ntchito zina za Yowasi ndi zonse zimene adazichita zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda. Nduna zake zidamchita chiwembu, ndipo zidamupha ku linga la Milo limene lili pa njira yotsikira ku Sila. Yosakara, mwana wa Simeati, ndi Yehozabadi, mwana wa Somere, ndiwo amene adachita zimenezi. Ndipo adakamuika m'manda momwe adaikidwa makolo ake mu mzinda wa Davide. Tsono Amaziya, mwana wake, adaloŵa ufumu m'malo mwake. Chaka cha 23 cha ufumu wa Yowasi, mwana wa Ahaziya mfumu ya ku Yuda, Yehowahazi mwana wa Yehu, adayamba kulamulira Aisraele ku Samariya, ndipo adakhala mfumu zaka 17. Iyeyo adachita zoipa kuchimwira Chauta. Zoipa zomwe Yerobowamu mwana wa Nebati adachimwitsa nazo Aisraele sadazileke ai. Nchifukwa chake Chauta adakwiyira Aisraele, ndipo kaŵirikaŵiri adalola kuti Hazaele mfumu ya ku Siriya ndiponso Benihadadi mwana wa Hazaeleyo aŵagonjetse. Tsono Yehowahazi adapemphera kwa Chauta ndipo Chauta adamumvera, poti adaona kupsinjidwa kwa Aisraele kumene mfumu ya ku Siriya idaŵapsinja nako. Nchifukwa chake Chauta adasankha mtsogoleri kuti apulumutse Aisraele m'manja mwa Asiriya. Motero Aisraele adakhala mwamtendere m'dziko mwao, monga momwe ankakhalira kale. Komabe Aisraelewo sadaleke kuchita zoipa zimene ankazichita anthu a pa banja la Yerobowamu, zimene iye ankachimwitsa nazo Aisraele. Aisraele adachitabe zoipazo, ndipo fano la Asera nalonso lidakhalabe ku Samariya. Nthaŵi imeneyo Yehowahazi analibe gulu lankhondo lalikulu. Anali ndi asilikali a pa akavalo makumi asanu okha, magaleta khumi ndiponso asilikali oyenda pansi zikwi khumi, popeza kuti mfumu ya ku Siriya inali itaononga asilikali ambiri nkuŵaponderezeratu ngati fumbi. Tsono ntchito zina za Yehowahazi pamodzi ndi zimene adazichita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele. Motero Yehowahazi adamwalira, naikidwa m'manda momwe adaikidwa makolo akewo ku Samariya. Tsono Yehowasi mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Chaka cha 37 cha ufumu wa Yowasi mfumu ya ku Yuda, Yehowasi mwana wa Yehowahazi adayamba kulamulira Aisraele ku Samariya, ndipo adalamulira zaka 16. Nayenso adachita zoipa kuchimwira Chauta. Sadaleke kuchita zoipa zonse zimene ankachita Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene adachimwitsa nazo Aisraele. Tsono ntchito zina za Yehowasi ndi zonse zimene adazichita, kudzanso zamphamvu zimene adaonetsa pomenyana nkhondo ndi Amaziya mfumu ya ku Yuda, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele. Motero Yehowasi adamwalira, naikidwa ku Samariya pamodzi ndi mafumu a ku Israele. Tsono Yerobowamu mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Masiku amenewo Elisa adadwala matenda ofa nawo, ndipo Yehowasi mfumu ya ku Israele adapita kukamzonda. Adakalira misozi pamaso pake nkumati, “Atate, atate! Magaleta a Israele ndiponso okwerapo ake!” Pamenepo Elisa adauza Yehowasi kuti, “Tengani uta ndi mivi yake.” Adatenga utawo ndi miviyo. Tsono Elisa adauza Yehowasi mfumu ya ku Israeleyo kuti, “Kokani utawu.” Iye nkukokadi. Apo Elisayo adaika manja ake pa manja a mfumuyo, ndipo adati, “Tsekulani windo lakuvuma.” Ndipo adatsekuladi. Tsono Elisa adati, “Ponyani.” Yehowasi nkuponya. Pomwepo Elisa adati, “Inuyo ndinu muvi wa Chauta wogonjetsera pa nkhondo, muvi wogonjetsera Asiriya. Pakuti mudzamenyana nawo nkhondo Asiriya ku Afeki mpaka kuŵatha onse.” Ndipo adati, “Tengani mivi inayo.” Yehowasi adaitenga. Tsono Elisa adauza mfumu ya ku Israele ija kuti, “Lasani pansi miviyo.” Ndipo iye adalasa pansi katatu, nkuleka. Tsono Elisa munthu wa Mulungu uja adazazira Yehowasiyo nati, “Mukadalasa kasanu kapena kasanu ndi kamodzi konse, mukadagonjetsa Asiriya mpaka kuŵatha onse. Koma tsopano mudzaŵagonjetsa katatu kokha.” Pambuyo pake Elisa adamwalira ndipo adamuika m'manda. Nthaŵi imeneyo magulu ankhondo a Amowabu ankathira nkhondo m'dzikomo chaka ndi chaka. Tsiku lina Aisraele ena kuti akaike mnzao ku manda, adangoona gulu lankhondo la Amowabuwo, iwo nkungoponya mtembowo m'manda mwa Elisa. Munthu wakufayo atangokhudza mafupa a Elisa, pomwepo adatsitsimuka nakhala chilili. Hazaele mfumu ya ku Siriya ankazunza Aisraele masiku onse a Yehowahazi. Koma Chauta adaŵakomera mtima Aisraelewo ndi kuŵamveranso chifundo. Adaŵalezera mtima chifukwa cha chipangano chimene Iye adaachita ndi Abrahamu, Isaki ndi Yakobe, choncho sadalole kuti adani aŵaononge. Ndipo sadaiŵale anthu akewo mpaka tsopano. Hazaele mfumu ya ku Siriya atamwalira, Benihadadi mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Nthaŵi imeneyo Yehowasi, mwana wa Yehowahazi, adalandanso kwa Benihadadi, mwana wa Hazaele, mizinda imene Benihadadiyo anali atailanda pomenyana nkhondo ndi Yehowahazi bambo wa Yehowasi. Yehowasi adagonjetsa Benihadadi katatu, nalandanso mizinda yonse ya Israele. Chaka chachiŵiri cha ufumu wa Yehowasi mwana wa Yehowahazi mfumu ya ku Israele, Amaziya mwana wa Yowasi, mfumu ya ku Yuda, adaloŵa ufumu. Iyeyo anali wa zaka 25 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 29 ku Yerusalemu. Mai wake anali Yehowadani wa ku Yerusalemu. Tsono Amaziya adachita zolungama pamaso pa Chauta, komabe osati nthaŵi zonse monga Davide kholo lake. Ankachita zonse monga m'mene ankachitira Yowasi bambo wake. Koma akachisi opembedzerako mafano pa zitunda sadaŵaononge. Anthu adapitirirabe kupereka nsembe ndi kumafukiza lubani pa malo amenewo. Atangolandira mphamvu zonse zaufumu m'manja mwake, Amaziya adapha anyamata ake amene adaapha mfumu ija, bambo wake. Koma ana a anthuwo sadaŵaphe, potsata zimene zidalembedwa m'malamulo a m'buku la Mose, m'mene Chauta adalamula kuti, “Atate sadzaphedwa chifukwa cha ana ao, kapena ana kuphedwa chifukwa cha atate ao. Koma aliyense adzafera machimo ake.” Tsono Amaziya adaphanso Aedomu okwanira 10,000 ku chigwa cha Mchere, nalanda mzinda wa Sela, ndipo adautchula dzina lakuti Yokitele, ndipo dzina lake ndi lomwelo mpaka pano. Nthaŵi ina Amaziya adatuma amithenga kwa Yehowasi mwana wa Yehowahazi, mdzukulu wa Yehu, mfumu ya ku Israele, kukanena momputa kuti, “Ubwere kuno, tidzaonane maso ndi maso.” Yehowasi, mfumu ya ku Israele, adabweza mau kwa Amaziya, mfumu ya ku Yuda, kuti, “Padangotere, mtungwi wa ku Lebanoni udaatumiza mau kwa mkungudza wa ku Lebanoni kuti, ‘Pereka mwana wako wamkazi kwa mwana wanga kuti amkwatire.’ Koma chilombo cha ku Lebanoni chidadzera pomwepo, nkuupondereza mtungwiwo. Inde iwe wagonjetsa Edomu, ndipo tsopano ukudzikuza. Badzitamira kupambana kwakoko, koma ai tsono khala kwanu komweko. Bwanji ukufuna kuutsa mavuto dala? Bwinotu ungagwe, iweyo pamodzi ndi anthu a ku Yuda.” Koma Amaziya sadasamaleko zimenezi. Motero Yehowasi mfumu ya ku Israele adapita kukamenyana nkhondo ndi Amaziya mfumu ya ku Yuda ku Betesemesi m'dziko la Yuda. Anthu a ku Yuda adagonjetsedwa ndi a ku Israele, ndipo wankhondo aliyense adathaŵira kwao. Tsono ku Betesemesiko Yehowasi, mfumu ya ku Israele, adagwirako Amaziya, mfumu ya ku Yuda, mwana wa Yowasi, mdzukulu wa Ahaziya, nabwera naye ku Yerusalemu. Ndipo Yehowasi adagumula khoma la Yerusalemu mamita 200, kuyambira ku chipata cha Efuremu mpaka ku chipata Chapangodya. Pamenepo adalanda golide ndi siliva yense, ndi ziŵiya zonse zimene adazipeza m'Nyumba ya Chauta ndi m'nyumba zosungira chuma cha mfumu. Adagwiranso anthu ena ngati chikole, nabwerera ku Samariya. Ntchito zina zonse za Yehowasi, makamaka za mphamvu zake, ndi za m'mene ankamenyerana nkhondo ndi Ahaziya mfumu ya ku Yuda, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele. Ndipo Yehowasi adamwalira naikidwa m'manda momwe adaikidwa makolo akewo, mafumu a ku Israele ku Samariya. Ndiye Yerobowamu mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Amaziya mwana wa Yowasi, mfumu ya ku Yuda, adakhala moyo zaka 15 atafa Yehowasi, mwana wa Yehowahazi, mfumu ya ku Israele. Tsono ntchito zina zonse zimene adachita Amaziya zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda. Ndiye kuti anthu ena adaapangana zomchita chiwembu Amaziyayo ku Yerusalemu, iye nkuthaŵira ku Lakisi. Adani akewo adatuma anthu omlondola, nakamphera komweko. Tsono adamtengera pa akavalo, nakamuika ku Yerusalemu m'manda momwe adaikidwa makolo ake mu mzinda wa Davide. Pamenepo anthu onse a ku Yuda adatenga Azariya, mwana wake, namlonga ufumu m'malo mwa Amaziya bambo wake. Azariyayo anali wa zaka 16 pamene adaloŵa ufumu. Azariya adagonjetsa mzinda wa Elati naumanganso nkuubwezera ku dziko la Yuda, bambo wake atamwalira. Chaka cha 15 cha ufumu wa Amaziya, mwana wa Yowasi, mfumu ya ku Yuda, Yerobowamu mwana wa Yehowasi, mfumu ya ku Israele, adaloŵa ufumu ku Samariya, ndipo adalamulira zaka 42. Iyeyo ankachita zoipa kuchimwira Chauta. Sadaleke kuchita zoipa zonse zimene ankachita kholo lake lija Yerobowamu, mwana wa Nebati, zimene adachimwitsa nazo Aisraele. Adalandanso madera ena amene kale anali a dziko la Israele, kuyambira ku chipata cha Hamati kumpoto mpaka kumwera kukafika ku Nyanja ya Araba. Motero zidachitikadi zimene Chauta, Mulungu wa Israele, adaalankhula kudzera mwa Yona mtumiki wake, mwana wa Amitai, mneneri wa ku Gatihefere. Chauta adaona kuti mavuto a Aisraele anali oopsa. Panalibe ndi mmodzi yemwe wotsala, kapolo kapena mfulu, woti angaŵathandize Aisraelewo. Koma Chauta sadaanena kuti adzafafaniza ufumu wa Israele pa dziko lapansi ai. Motero adaŵapulumutsa Aisraele kudzera mwa Yerobowamu mwana wa Yehowasi. Tsono ntchito zina zonse za Yerobowamu, makamaka za mphamvu zake, za m'mene ankamenyera nkhondo, ndiponso za m'mene adagonjetsera mzinda wa Damasiko ndi wa Hamati naibwezeranso mizindayo ku Israele, zonsezo zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele. Ndipo Yerobowamu adamwalira, naikidwa m'manda momwe adaikidwa makolo akewo, mafumu a ku Israele. Tsono Zekariya mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Chaka cha 27 cha ufumu wa Yerobowamu mfumu ya ku Israele, Azariya mwana wa Amaziya mfumu ya ku Yuda, adaloŵa ufumu. Iyeyu anali wa zaka 16 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 52 ku Yerusalemu. Mai wake anali Yekoliya wa ku Yerusalemu. Azariya adachita zolungama pamaso pa Chauta, monga momwe ankachitira bambo wake Amaziya. Komabe akachisi opembedzerako mafano pa zitunda sadaŵaononge. Anthu ankaperekabe nsembe ndi kumafukiza lubani pa malo amenewo. Tsono Chauta adailanga mfumuyo ndi nthenda ya khate mpaka kufa kwake, ndipo inkakhala m'nyumba yakeyake yapadera. Choncho Yotamu mwana wa mfumuyo ndiye amene ankayang'anira banja la mfumu, namalamulira anthu m'dzikomo m'malo mwake. Tsono ntchito zina za Azariya ndi zonse zimene adazichita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda. Ndipo adamwalira naikidwa m'manda momwe adaikidwa makolo akewo mu mzinda wa Davide. Ndiye Yotamu mwana wake adaloŵa ufumu. Chaka cha 38 cha ufumu wa Azariya mfumu ya ku Yuda, Zekariya mwana wa Yerobowamu, adaloŵa ufumu wa Aisraele ku Samariya kwa miyezi isanu ndi umodzi. Iyeyo ankachita zoipa kuchimwira Chauta, monga momwe ankachitira makolo ake. Sadazileke zoipa zimene Yerobowamu mwana wa Nebati, adachimwitsa nazo Aisraele. Tsono Salumu mwana wa Yabesi adamchita chiwembu Zekariya, ndipo adamphera ku Ibleamu. Choncho Salumuyo adaloŵa ufumu m'malo mwake. Tsono ntchito zonse zimene adachita Zekariya zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a Israele. Izi ndi zimene Chauta adalonjeza Yehu, adati, “Ana ako aamuna adzalamulira Aisraele mpaka mbadwo wachinai.” Ndipo zidachitikadi momwemo. Salumu mwana wa Yabesi adaloŵa ufumu pa chaka cha 39 cha ufumu wa Uziya mfumu ya ku Yuda, ndipo adalamulira mwezi umodzi ku Samariya. Tsono Menahemu mwana wa Gadi, adachoka ku Tiriza nakafika ku Samariya. Adapha Salumu mwana wa Yabesi ku Samariyako, iyeyo nkuloŵa ufumu m'malo mwa Salumu. Tsono ntchito zonse za Salumu ndi chiwembu chimene adachita, zonsezi zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele. Nthaŵi imeneyo, kuchokera ku Tiriza Menahemu adakaononga mzinda wa Tapuwa ndi anthu onse amene anali m'menemo, kuphatikiza dziko lonse lozungulira, poti iwo sadamgonjere. Adaphanso akazi apathupi amumzindamo naŵang'amba. Chaka cha 39 cha ufumu wa Azariya mfumu ya ku Yuda, Menahemu mwana wa Gadi adaloŵa ufumu wa ku Israele, ndipo adalamulira zaka khumi ku Samariya. Menahemu ankachita zoipa kuchimwira Chauta. Masiku onse a moyo wake sadaleke kuchita zoipa zonse zimene ankachita Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene adachimwitsa nazo Aisraele. Pambuyo pake Pulo, mfumu ya ku Asiriya, adadzathira nkhondo dziko la Israele. Ndipo Menahemu adakapereka kwa Pulo siliva wokwanira makilogramu 34,000, kuti Puloyo amthandize kukhazikitsa ufumu wake. Menahemu adapeza ndalamazo kuchokera ku msonkho umene ankakhometsa Aisraele. Anthu onse olemera ankaŵakhometsa aliyense masekeli asiliva makumi asanu. Motero mfumu ya ku Asiriya idabwerera, ndipo sidakhale m'dzikomo. Tsono ntchito zina za Menahemu, ndi zonse zimene adazichita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele. Ndipo Menahemu adamwalira, naikidwa m'manda momwe adaikidwa makolo akewo. Tsono Pekahiya mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Chaka cha 50 cha ufumu wa Azariya mfumu ya ku Yuda, Pekahiya mwana wa Menahemu, adaloŵa ufumu wa ku Israele ku Samariya, ndipo adalamulira zaka ziŵiri. Pekahiya adachita zoipa kuchimwira Chauta. Sadaleke kuchita zoipa zimene ankachita Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene adachimwitsa nazo Aisraele. Tsono Peka mwana wa Remaliya nduna yake, pamodzi ndi anthu makumi asanu a ku Giliyadi, adapangana za chiwembu napha Pekahiya ku Samariya m'chipinda choteteza nyumba ya mfumu. Pambuyo pake Pekayo adaloŵa ufumu m'malo mwake. Tsono ntchito zina za Pekahiya ndi zonse zimene adazichita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele. Chaka cha 52 cha ufumu wa Azariya mfumu ya ku Yuda, Peka mwana wa Remaliya adaloŵa ufumu wa ku Israele ku Samariya. Ndipo adalamulira zaka makumi aŵiri. Koma adachita zoipa kuchimwira Chauta. Sadaleke kuchita zoipa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene adachimwitsa nazo Aisraele. Nthaŵi ya Peka mfumu ya ku Israele, Tigilati-Pilesere mfumu ya ku Asiriya, adadzagonjetsa mizinda iyi: Iyoni, Abele-Beti-Maaka, Yanowa, Kedesi, Hazori, dziko la Giliyadi ndi la Galilea, ndiponso dziko lonse la Nafutali. Ndipo anthu onse am'menemo adaŵagwira ukapolo, napita nawo ku Asiriya. Nthaŵi imeneyo Hoseya mwana wa Ela adachita chiwembu kuchitira mfumu Peka, namupha. Ndipo iyeyo adaloŵa ufumu m'malo mwake pa chaka cha 20 cha ufumu wa Yotamu mwana wa Uziya mfumu ya ku Yuda. Tsono ntchito zina za Peka ndi zonse zimene adazichita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a Israele. Chaka chachiŵiri cha ufumu wa Peka mwana wa Remaliya, mfumu ya ku Israele, Yotamu mwana wa Uziya mfumu ya ku Yuda, adaloŵa ufumu. Anali wa zaka 25 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 16 ku Yerusalemu. Mai wake anali Yerusa, mwana wa Zadoki. Yotamu adachita zolungama pamaso pa Chauta ndipo kutsata zonse zimene ankachita Uziya bambo wake. Komabe akachisi opembedzerako mafano pa zitunda sadaŵaononge. Anthu ankaperekabe nsembe namafukiza lubani pa malo amenewo. Yotamu ndiye adamanga chipata chakumpoto cha Nyumba ya Chauta. Tsono ntchito zina za Yotamu, ndi zonse zimene ankachita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda. Nthaŵi imene Yotamu ankalamulira, mpamene Chauta adayambapo kutuma Rezini mfumu ya ku Siriya ndi Peka mwana wa mfumu ya ku Israele, kuti akathire nkhondo dziko la Yuda. Yotamu adamwalira, naikidwa m'manda momwe adaikidwa makolo akewo, mu mzinda wa Davide kholo lake. Ndipo Ahazi mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Chaka cha 17 cha ufumu wa Peka mwana wa Remaliya, Ahazi mwana wa Yotamu mfumu ya ku Yuda, adaloŵa ufumu. Ahazi anali wa zaka 20 pamene adaloŵa ufumu ndipo adalamulira zaka 16 ku Yerusalemu. Iyeyo sadachite zolungama pamaso pa Chauta monga m'mene Davide kholo lake ankachitira. Koma adatsata zitsanzo zoipa za mafumu a ku Israele. Adapereka mwana wake wamwamuna ngati nsembe yopsereza potsatira miyambo yonyansa ya anthu a mitundu ina imene Chauta adaaipirikitsa m'dzikomo pamene ankafika Aisraele. Ndipo ankapereka nsembe ndi namafukiza lubani ku akachisi opembedzerako mafano, pa mapiri ndi patsinde pa mtengo uliwonse wogudira. Tsono Rezini mfumu ya ku Siriya ndi Peka mwana wa Remaliya mfumu ya ku Israele adabwera kudzathira nkhondo Yerusalemu namzinga Ahazi ndi zithando zankhondo, koma sadathe kumgonjetsa. Nthaŵi imeneyo Rezini mfumu ya ku Edomu adapirikitsa Ayuda ku Elati, nalanda mzindawo, kuubwezera kwa Aedomu, ndipo iwo adakhala kumeneko mpaka lero lino. Pamenepo Ahazi adatuma amithenga kwa Tigilati-Pilesere mfumu ya ku Asiriya kukanena kuti, “Ine ndine mwana wanu ndiponso mtumiki wanu. Bwerani mudzandipulumutse kwa mfumu ya ku Siriya ndi kwa mfumu ya ku Israele, amene akundithira nkhondo.” Ndipo Ahazi adatenga siliva ndi golide amene adampeza m'Nyumba ya Chauta ndi mosungira chuma cha ku nyumba ya mfumu, namtumiza kwa mfumu ya ku Asiriya kuti zikhale ngati mphatso. Tsono mfumu ya ku Asiriya idamvera Ahazi ndipo idakathira nkhondo Damasiko nilanda mzindawo ndi kupha Rezini. Anthu ake idaŵatenga ukapolo kupita nawo ku Kiri. Pamene mfumu Ahazi adapita ku Damasiko kuti akakumane ndi Tigilati-Pilesere mfumu ya ku Asiriya, adaonako guwa kumeneko. Tsono adatumizira wansembe Uriya chitsanzo chake cha guwalo ndi maonekedwe ake, osasiyapo nkanthu komwe. Ndiye wansembe Uriya adamanga guwalo, Mfumu Ahazi asanafike kuchokera ku Damasiko. Adalimanga potsata chitsanzo chimene Ahazi adaatumiza kuchokera ku Damasiko. Mfumu itabwera kuchokera ku Damasiko, nipenya guwa lija, idasendera pafupi ndi guwalo ndi kukwera kuguwako. Tsono mfumuyo idapereka nsembe yopsereza ndi chopereka cha chakudya. Idathiranso nsembe yake yachakumwa, ndipo idawaza magazi a nsembe yake yamtendere paguwapo. Kenaka mfumu Ahazi adachotsa guwa lamkuŵa limene linali lomangira Chauta, pakati pa guwa lake ndi Nyumba ya Chauta, ndipo adalisuntha nakalikhazika chakumpoto kwa guwa lakelo. Kenaka mfumuyo idalamula wansembe kuti, “Pa guwa lalikululo uperekepo nsembe zopsereza zam'maŵa, ndiponso chopereka chamadzulo cha chakudya. Uziperekanso nsembe zopsereza ndi nsembe zaufa za mfumu, ndiponso za anthu a m'dziko monsemo, pamodzi ndi zopereka za chakumwa. Ndipo pa nsembezo uwazepo magazi onse a nsembe zopsereza ndi a nsembe zonse. Koma guwa lamkuŵalo ndidzaligwiritsa ntchito poombeza.” Tsono wansembe Uriya adachita zonsezo, monga momwe mfumu Ahazi adaalamulira. Pambuyo pake mfumu Ahazi adamasula mafulemu a maphaka, nachotsapo beseni. Ndipo chimbiya chimene chinali pamwamba pa ng'ombe zamkuŵa adachitsitsa ndi kuchikhazika pa maziko amiyala. Ndipo chifukwa chofuna kukondweretsa mfumu ya ku Asiriya, adachotsa kadenga ka pamwamba pa mpando waufumu kamene anali atakamanga m'kati mwa Nyumba ya Chauta, ndiponso adatseka khomo la panja pamene mfumu inkaloŵera m'Nyumbamo. Tsono ntchito zina za Ahazi pamodzi ndi zonse zimene adazichita zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda. Ahazi adamwalira, naikidwa m'manda mu mzinda wa Davide. Ndipo Hezekiya mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Chaka cha 12 cha ufumu wa Ahazi mfumu ya ku Yuda, Hoseya mwana wa Ela adaloŵa ufumu wa ku Israele ku Samariya. Ndipo adalamulira zaka zisanu ndi zinai. Tsono adachita zoipa kuchimwira Chauta, komabe osalingana ndi mafumu a ku Israele amene ankalamulira, iyeyo asanaloŵe ufumu. Salimanezere, mfumu ya ku Asiriya, adadza kudzamthira nkhondo, ndipo Hoseya adamgonjera, namakhoma msonkho kwa iyeyo. Koma tsiku lina mfumu ya ku Asiriya idaona kuti Hoseya akuchita zaupandu. Ndiye kuti Hoseyayo anali atatuma amithenga kukapempha chithandizo kwa So, mfumu ya ku Ejipito, Ndiponso adaaleka kukhoma msonkho kwa mfumu ya ku Asiriya, m'menemo kale ankakhoma chaka ndi chaka. Nchifukwa chake mfumu ya ku Asiriya itamva zimenezi, idamanga Hoseya ndi kumuika m'ndende. Nthaŵi yomweyo Salimanezere, mfumu ya ku Asiriya, adathira nkhondo dziko la Israele nakafika ku Samariya, nkukauzinga mzindawo ndi zithando zankhondo zaka zitatu. Chaka chachisanu ndi chinai cha ufumu wa Hoseya, mfumu ya ku Asiriya idagonjetsa Samariya, ndipo idatenga Aisraele kuŵachotsa kwao kupita nawo ku Asiriya. Idaŵakhazika ena ku mzinda wa Hala, ena kufupi ndi mtsinje wa Habori m'dera la Gozani, ndipo enanso ku mizinda ya Amedi. Zimenezo zidaoneka chifukwa Aisraele adachimwira Chauta Mulungu wao, amene adaŵatulutsa ku dziko la Ejipito, kuŵachotsa m'manja mwa Farao mfumu ya ku Ejipito. Aisraelewo ankapembedza milungu ina, ndipo ankayenda motsata miyambo ya anthu a mitundu ina amene Chauta adaŵapirikitsa pamene ankafika Aisraele. Ankatsatanso miyambo yachilendo imene mafumu ena a Aisraele anali ataiyambitsa. Ndipo Aisraele ankachita zinthu zoipa mobisika namachimwira Chauta Mulungu wao. Adadzimangira akachisi opembedzerako mafano ku midzi yao yonse ndi ku mizinda yomwe. Adadzimangira zipilala zoimiritsa ndiponso mafano pa phiri lililonse lalitali ndi patsinde pa mitengo yogudira. Ndipo anthuwo ankafukiza lubani ku akachisi onse, monga m'mene ankachitira anthu a mitundu ina amene Chauta adaŵapirikitsa m'dzikomo pamene ankafika Aisraelewo. Tsono adapembedza mafano kuchimwira Chauta amene anali ataŵauza kuti, “Musadzachite zimenezi.” Monsemo Chauta adatuma amithenga ndi aneneri ake ku Israele ndi ku Yuda, okalalika kuti, “Musinthe makhalidwe anu auchimo ndipo mumvere Malamulo anga amene ndidaŵapereka kwa makolo anu, kudzera mwa aneneri, atumiki anga.” Koma anthuwo sankamva, anali ouma mitu monga momwe analiri makolo ao amene sadakhulupirire Chauta Mulungu wao. Iwowo adanyoza malamulo a Chauta ndi chipangano cha Chauta chimene Iye adachita ndi makolo ao. Adanyozanso zochenjeza za Chauta. Adatsata milungu yachabechabe, ndipo iwo omwe adasanduka achabechabe. Ankatsata zitsanzo za anthu a mitundu ina okhala nawo pafupi, ngakhale Chauta anali atalamula kuti asamachite mofanana ndi mitundu imeneyo. Motero adasiya malamulo onse a Chauta Mulungu wao, nadzipangira mafano aŵiri osungunula anaang'ombe. Adapanganso mafano ena a Asera namapembedza zinthu zakumlengalenga ndiponso Baala. Anthuwo adapereka ngati nsembe ana ao aamuna ndi ana ao aakazi, ndipo ankaombeza maula, namachitanso zanyanga. Adadzipereka kuti azichita zoipa zochimwira Chauta, namkwiyitsa. Nchifukwa chake Chauta adakwiya nawo kwambiri Aisraele, ndipo adaŵachotsa osafuna kuŵaonanso. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adatsalako, kupatula a fuko la Yuda okha. Nawonso a fuko la Yuda sadasunge malamulo a Chauta Mulungu wao, koma ankayenda motsata miyambo imene Aisraele adaiyambitsa. Choncho Chauta adakana zidzukulu zonse za Aisraele, nazizunza, nkuzipereka mu ulamuliro wa anthu ofunkha, mpaka ataŵachotseratu onse. Chauta ataŵalekanitsa Aisraele kuŵachotsa pa banja la Davide, iwo adaika Yerobowamu mwana wa Nebati kuti akhale mfumu yao. Yerobowamuyo adaletsa Aisraele kuti asatsate Chauta, ndipo adaŵachimwitsa kwambiri Aisraelewo. Aisraele ankachita zoipa zonse zimene adachita Yerobowamu mfumu yao. Sadaleke zimenezo, mpaka Chauta adaŵachotsa Aisraele kotheratu, monga momwe adaalankhulira kudzera mwa atumiki ake onse, aneneri. Motero Aisraele adatengedwa ukapolo kuchoka ku dziko lakwao kupita ku Asiriya, ndipo ali kumeneko mpaka pano. Pambuyo pake mfumu ya ku Asiriya idabwera ndi anthu kuchokera ku mizinda ya Babiloni, Ava, Hamati ndi Sefaravaimu, nkudzaŵakhazika ku dziko la Samariya m'malo mwa Aisraele amene adatengedwa ukapolo. Tsono anthuwo adaloŵa m'midzi ya Samariyayo naisandutsa yaoyao. Koma iwowo chiloŵere chao kumeneko sankapembedza Chauta. Nchifukwa chake Chauta adatumiza mikango pakati pao, nipha ena mwa iwowo. Motero mfumu ya ku Asiriya idamva kuti, “Anthu a mitundu ina aja amene mudaŵakhazika m'midzi ya ku Samariya, sakudziŵa kupembedza Mulungu wa dzikolo. Nchifukwa chake Mulungu adaŵatumizira mikango pakati pao, ndipo ikuŵapha, chifukwa sakuchita zimene Mulunguyo akufuna.” Tsono mfumu ya ku Aasiriya idalamula kuti, “Tumani mmodzi mwa ansembe amene mudaŵagwira kumeneko, akakhale komweko, kuti akaŵaphunzitse kupembedza Mulungu wa dzikolo.” Motero mmodzi mwa ansembe amene adaŵatenga ku Samariya adadzakhala ku Betele, nayamba kuŵaphunzitsa anthu kupembedza Chauta. Koma mtundu uliwonse wa anthuwo unkapangabe mafano a milungu yaoyao, ndipo ankaika milunguyo m'nyumba zachipembedzo zimene Asamariya adaazimanga. Mtundu uliwonse wa anthuwo unali ndi nyumba za mulungu wao ku mzinda uliwonse kumene ankakhala. Anthu a ku Babiloni adadzipangira fano lotchedwa Sukoti-Benoti. Anthu a ku Kuta adapanga fano lotchedwa Neregali, anthu a ku Hamati adapanga fano lotchedwa Ashima. Aavi adapanga fano lotchedwa Nibihazi ndiponso Taritaki. Asefaravaimu ankapereka ana ao ngati nsembe zopsereza kwa Adrameleki ndi kwa Anameleki, milungu ya Asefaravaimu. Anthuwo ankapembedzanso Chauta nadzisankhira pakati pao anthu wamba, kuti akhale ansembe otumikira ku nyumba zao zachipembedzo. Ansembe amenewo ndi amene ankaperekera anthu nsembe m'nyumba zopembedzeramo milungu yao ku zitunda. Motero ankapembedza Chauta, kwinaku ankatumikirabe milungu yao, potsata makhalidwe a mitundu ya anthu a kumene adatengedwa ukapoloko. Akuchitabe zimene ankachita kale mpaka lero lino. Iwowo salemekeza Chauta kwenikweni ndipo satsata zogamula kapena zolengeza, ngakhale malangizo kapena malamulo amene Chauta adalamula zidzukulu za Yakobe, amene adamtchula kuti Israele. Chauta adaachita nawo Aisraele chipangano naŵalamula kuti, “Musapembedze milungu ina kapena kuilambira kapena kuitumikira, kapena kuiperekera nsembe. Koma muzipembedza Ine Chauta amene ndidakutulutsani ku dziko la Ejipito ndi mphamvu zanga zazikulu ndi mkono wanga wokutetezani. Muzigwadira Ine Chauta, ndipo muzipereka nsembe kwa Ine ndekha. Ndipo inu muzisamala zogamula ndi zolengeza, malangizo ndi malamulo amene Ine Chauta ndidakupatsani. Musamapembedza milungu ina ai, ndipo musaiŵale chipangano chimene ndidachita ndi inu. Musamapembedze milungu ina, koma muzipembedza Ine Chauta Mulungu wanu, ndipo ndidzakupulumutsani kwa adani anu.” Komabe iwowo sankamva zimenezi, koma ankachitabe zimene adakhala akuchita kuyambira kale. Motero mitundu ya anthu imeneyi inkapembedza Chauta, kwinaku nkumatumikira milungu yao yachabechabe ija. Ana ao adachitanso zomwezo, adzukulu ao adachita zokhazokhazo zimene ankachita makolo ao, ndipo akuchitabe zomwezo mpaka pano. Chaka chachitatu cha ufumu wa Hoseya, mwana wa Ela, mfumu ya ku Israele, Hezekiya, mwana wa Ahazi, mfumu ya ku Yuda, adaloŵa ufumu. Anali wa zaka 25 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 29 ku Yerusalemu. Mai wake anali Abi, mwana wa Zekariya. Hezekiya adachita zolungama pamaso pa Chauta, monga momwe ankachitira Davide kholo lake. Adaononga akachisi onse opembedzerako mafano, nagwetsa zipilala zamiyala, nkuthyolanso mitengo ya Asera. Kenaka adatswanya njoka yamkuŵa ija imene adapanga Mose, popeza kuti mpaka masiku amenewo, Aisraele ankaifukizira lubani pofuna kuilemekeza njokayo. Ankaitchula kuti Nehusitani. Hezekiyayo adakhulupirira Chauta, Mulungu wa Aisraele, kotero kuti panalibe wofanafana naye pakati pa mafumu onse a ku Yuda iyeyo atafa, ngakhale pakati pa amene analipo kale iye asanaloŵe ufumu. Iyeyo ankakangamira kwa Chauta. Sadaleke kutsata Chauta, koma ankasunga malamulo amene Iye adapatsa Mose. Nchifukwa chake Chauta anali naye. Kulikonse kumene ankapita, zinthu zinkamuyendera bwino. Hezekiyayo adapandukira mfumu ya ku Asiriya, mwakuti sankaitumikiranso ai. Adakantha Afilisti mpaka ku Gaza ndi ku dera lake lonse. Adaononga mudzi uliwonse ndi mzinda uliwonse. Chaka chachinai cha ufumu wa Hezekiya chimene chinali chachisanu ndi chiŵiri cha ufumu wa Hoseya, mwana wa Ela, mfumu ya ku Israele, Salimanezere mfumu ya ku Asiriya adabwera kudzathira nkhondo mzinda wa Samariya, ndipo adauzinga ndi zithando zankhondo. Tsono adaulanda patapita zaka zitatu. Chaka chachisanu ndi chimodzi cha ufumu wa Hezekiya chimene chinali cha chisanu ndi chinai cha ufumu wa Hoseya, mfumu ya ku Israele, mzinda wa Samariya udalandidwa. Mfumu ya ku Asiriya idatenga Aisraele kupita nawo ku ukapolo ku Asiriya. Adakaŵakhazika ku mzinda wa Hala, ndinso pafupi ndi mtsinje wa Habori m'dera la Gozani, ndi ku mizinda ya Amedi. Izi zidachitika chifukwa choti anthuwo sadamvere mau a Chauta Mulungu wao, koma adaphwanya chipangano chake, pamodzi ndi zonse zimene Mose mtumiki wa Chauta adaŵalamula. Sadatsate zimenezo kapena kuzigwiritsa ntchito. Chaka cha 14 cha ufumu wa Hezekiya, Senakeribu mfumu ya ku Asiriya adadzathira nkhondo mizinda yonse yamalinga ya ku Yuda nailanda. Ndipo Hezekiya mfumu ya ku Yuda adatumiza mau ku Lakisi kwa mfumu ya ku Asiriya, onena kuti, “Ndidalakwa ine. Lekeni. Chilichonse chimene munene ndidzachita.” Pamenepo mfumu ya ku Asiriya idamlamula Hezekiya, mfumu ya ku Yuda, kuti azipereka makilogramu a siliva okwanira 3,000 ndi makilogramu a golide 1,000. Tsono Hezekiya adapereka kwa mfumuyo siliva yense wa ku Nyumba ya Chauta, pamodzi ndi wa ku nyumba zosungira chuma cha mfumu. Nthaŵi imeneyo mpamene Hezekiya adakanganula golide wa pa zitseko za Nyumba ya Chauta ndi wa pa mphuthu za makomo, amene iye yemweyo anali atamatapo. Tsono Hezekiyayo adapereka golideyo kwa mfumu ya ku Asiriya. Komabe mfumu ya ku Asiriya idatuma mtsogoleri wankhondo, nduna yaikulu ndi kazembe wankhondo, pamodzi ndi gulu lankhondo lalikulu kwa mfumu Hezekiya ku Yerusalemu kuchokera ku Lakisi. Iwowo adapita nakafika ku Yerusalemu, ndipo adakaima pafupi ndi ngalande yamadzi yochokera ku dziŵe lakumtunda, pa mseu waukulu wopita ku malo a mmisiri wa nsalu. Pamenepo iwo adaitana mfumu, ndipo anthu atatu adatuluka mu mzinda nakakumana nawo. Anthu aŵa: mkulu woyang'anira nyumba ya mfumu, dzina lake Eliyakimu mwana wa Hilikiya, Sebina mlembi wa bwalo, ndi Yowa mwana wa Asafu, wolemba zochitika. Kazembe wankhondo uja adaŵauza kuti akanene kwa Hezekiya mau aŵa: “Mfumu yaikulu, mfumu ya ku Asiriya, ikuti, ‘Chimene chikulimbitsa chikhulupiriro chako motere nchiyani? Kodi ukuganiza kuti mau okha nkulingana ndi luso ndi mphamvu pa nkhondo? Kodi tsono ukudalira yani kuti uzindigalukira? Makamaka ukuyembekeza kuti Ejipito adzakuthandiza ati. Koma kuteroko kuli ngati kukhulupirira bango lothyoka limene litha kumbaya munthu m'manja ataliyesa ndodo yoyendera. Ndimo m'mene mfumu ya ku Ejipito imamchitira aliyense woidalira. “ ‘Kapena undiwuza kuti mumakhulupirira Chauta Mulungu wanu. Kodi si Mulungu yemweyo amene akachisi ake ndi maguwa ake Hezekiya adaŵathetsa, nauza anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti, “Muzipembedza pa guwa ili la ku Yerusalemu?” Tiye tsono utembezane ndi mbuye wanga, mfumu ya ku Asiriya: Ndidzakupatsa akavalo okwanira zikwi ziŵiri, ngati iwe ungathe kupeza anthu ake okwerapo. Ungathe bwanji kupambana ngakhale mmodzi yekha mwa akazembe ang'onoang'ono a mbuye wanga, pamene ukukhulupirira Aejipito, kuti akupatse magaleta ndi anthu okwera pa akavalo? Ndiponso kodi sukudziŵa kuti ndi Chauta amene wandibweretsa kuno, kuti ndidzathire nkhondo dziko lino ndi kuliwononga? Chautayo ndiye adachita kundiwuza kuti ndilimbane nalo ndi kuliwononga dziko lano.’ ” Pamenepo Eliyakimu, mwana wa Hilikiya, ndiponso Sebina ndi Yowa adauza kazembeyo kuti, “Pepani, mutilankhule m'Chiaramu atumiki anufe, poti timachimvetsa. Musatilankhule m'Chiyuda pakuti anthu onse ali pakhomaŵa alikumva.” Koma kazembe uja adati, “Kodi mukuganiza kuti mfumu yanga idandituma kuti ndilankhule mau ameneŵa kwa inu nokha ndi kwa mfumu yanu basi? Iyai, ndikulankhulanso kwa anthu amene akhala pakhomawo, amene adzayenera kudya ndoŵe yao yomwe ndi kumwa mkodzo wao womwe, monga momwe mudzachitire inuyo.” Tsono kazembe uja adaimirira nafuula m'Chiyuda kuti, “Mverani mau a mfumu yaikulu, mfumu ya ku Asiriya. Mfumuyo ikuti, Musalole kuti Hezekiya akunyengeni, chifukwa sadzatha kukupulumutsani m'manja mwanga. Asakukakamizeni kuti mudalire Chauta pokuuzani kuti mosapeneka konse Chauta wanuyo adzakupulumutsani, ndipo kuti mfumu ya ku Asiriya sidzalanda mzinda wanuwu. Musamumvere Hezekiya. Mfumu ya ku Asiriya ikukulamulani kuti mutulukemo mumzindamo, ndipo muigonjere. Mukatero, aliyense mwa inu azidzadya mphesa ndi nkhuyu zake ndi kumamwa madzi a m'chitsime chake. Mudzachita choncho mpaka nthaŵi imene mfumuyo idzakutengeni kupita nanu ku dziko lolingana ndi lanuli, dziko la chonde la mwana alirenji, kuti kumeneko mudzakhale moyo, osafa. Ndiye inu chenjerani, Hezekiya asakupusitseni pokuuzani kuti Chauta adzakupulumutsani. Mwa milungu ya anthu a mitundu ina, kodi alipo ndi mmodzi yemwe amene adapulumutsapo dziko lake kwa mfumu ya ku Asiriya? Kodi milungu ya Hamati ndi Aripadi ili kuti? Nanga milungu ya Sefaravaimu, Hena ndi Iva ili kuti? Kodi milunguyo idaupulumutsa mzinda wa Samariya kwa mbuye wanga? Kodi ndi iti mwa milungu yonse ya maikoŵa imene idapulumutsapo maiko ao kwa mfumu yathu, kuti inu muziti Chauta nkupulumutsa Yerusalemu kwa mfumu yathuyo?” Koma anthu adangokhala chete, osayankhapo kanthu chifukwa mfumu Hezekiya adaaŵalamula kuti, “Musamuyankhe ai.” Tsono Eliyakimu mwana wa Hilikiya, amene ankayang'anira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo, ndi Yowa mwana wa Asafu, wolemba zochitika, adang'amba zovala zao mwachisoni, ndipo adapita kwa mfumu Hezekiya nakamuuza zimene kazembe wa ku Asiriya uja adaalankhula. Hezekiya atangomva zimenezi, adang'amba zovala zake mwachisoni, ndipo adavala chiguduli, nakaloŵa m'Nyumba ya Chauta. Tsono adatuma Eliyakimu mkulu wa nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa mfumu, ndiponso ansembe akuluakulu, onse atavala ziguduli, kuti apite kwa mneneri Yesaya, mwana wa Amozi. Iwowo adauza Yesaya mau a Hezekiya onena kuti, “Lero ndi tsiku la mavuto, la chilango ndi la manyazi. Tili ngati mkazi amene ali pafupi kubala mwana, koma alibe mphamvu zombalira mwanayo. Mfumu ya ku Asiriya yatuma kazembe wake wankhondo kudzanyoza Mulungu wamoyo. Makamaka Chauta, Mulungu wanu, wamva kunyoza kumeneku, ndipo adzaŵalanga anthu amene adamunyozawo. Nchifukwa chake muŵapempherere anthu otsalaŵa amene akali ndi moyo.” Pamene Yesaya adamva mau a mfumu Hezekiyawo, adati, “Kauzeni mbuyanu mau a Chauta akuti, ‘Usade nawo nkhaŵa mau ondinyoza a atumiki a mfumu ya ku Asiriya. Ndidzaika mumtima mwa mfumuyo ganizo lina lakuti ikadzangomva mphekesera, idzaumirizidwa kubwerera ku dziko lake, ndipo Ine ndidzamphetsa kwao komweko.’ ” Kazembe wankhondo uja adamva kuti mfumu ya ku Asiriya ija inachoka ku Lakisi, ndipo inali kuchita nkhondo ndi mzinda wa Libina. Motero anapita kumeneko kukakambirana nayo. Tsono pamene mfumu ya ku Asiriya idamva kuti mfumu Tirihaka wa ku Etiopiya akubwera kudzachita nayo nkhondo, idatumanso amithenga kwa Hezekiya ndi mau onena kuti, “Mulungu wako amene ukumkhulupirirayo asakunyenge pokulonjeza kuti Yerusalemu sadzagwa m'manja mwa ine mfumu ya ku Asiriya. Wakhala ulikumva zimene mafumu a ku Asiriya adaŵachita maiko onse, kuti adaŵaononga kotheratu. Tsono iweyo ndiye nkupulumuka? Makolo anga adaononga mizinda ya Gozani, Harani ndi Rezefe. Ndipo adapha anthu a ku Edeni amene ankakhala ku Telasara. Kodi milungu ya anthu a mitundu inawo idaŵapulumutsa? Nanga mafumu a m'mizinda ya Hamati, Aripadi, Separavaimu ndi Iva ali kuti?” Mfumu Hezekiya adalandira kalata kwa amithenga aja, naiŵerenga. Pomwepo adapita ku Nyumba ya Chauta naika kalatayo m'menemo pamaso pa Chauta. Tsono adapemphera kwa Chauta kuti, “Inu Chauta, Mulungu wa Israele, amene mumakhala pa mpando wanu waufumu pamwamba pa akerubi, Inu nokha ndinu Mulungu wolamulira mafumu onse a dziko lonse lapansi. Mudalenga dziko lakumwamba ndi dziko lapansi. Tsono Inu Chauta, tcherani khutu, mumve. Inu Chauta, tsekulani maso, muwone. Mumve mau onse amene Senakeribu adalankhula, onyoza Inu Mulungu wamoyo. Inu Chauta, zoonadi mafumu a ku Asiriya adaononga anthu a mitundu ina yonse, nasandutsa maiko ao chipululu. Adatentha milungu yao imene siinali milungu konse, koma mafano amitengo ndi amiyala opangidwa ndi anthu, nchifukwa chake adaiwononga. Ndiye Inu Chauta, Mulungu wathu, ndikukupemphani kuti mutipulumutse kwa munthu ameneyu, kuti mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadziŵe kuti Inu nokha, Chauta, ndiye Mulungu.” Tsono Yesaya mwana wa Amozi adatumiza kwa mfumu Hezekiya mau omuuza kuti Chauta, Mulungu wa Israele, wamva pemphero lake lija lonena za Senakeribu mfumu ya ku Asiriya. Poitsutsa mfumuyo Chauta adati, “Mzinda wa Ziyoni ukukunyoza ndi kukuseka, iwe Senakeribu, mzinda wa Yerusalemu ukupukusa mutu kumbuyo kwako monyodola. “Kodi iwe wanyoza ndi kulalatira yani? Kodi ndani amene wamufuulira ndi kumuyang'ana monyada? Si wina ai, koma Woyera uja wa Israele! Udatuma amithenga ako kudzandinyoza Ine, ndipo udati, ‘Ndi magareta anga ochuluka ndidakwera mapiri ataliatali, ndidafika mpaka pa nsonga za mapiri a ku Lebanoni. Ndidagwetsa mitengo yake ya mkungudza yaitali kwambiri, ndiponso mitengo yake ya paini yabwino koposa. Ndidaloŵanso m'kati mwake mwenimweni, m'nkhalango yake yoŵirira kwabasi. Ndidakumba zitsime ku maiko achilendo ndi kumwamo madzi. Ndi mapazi anga ndidapondereza ndi kuumitsa mitsinje ya ku Ejipito.’ “Koma Ine Chauta ndikuti, Kodi sudamvepo kuti zimenezi ndidazikonzeratu kalekale? Ndidaaziganiziratu masiku amakedzana, tsopano ndazichitadi. Iweyo kwako kunali kungogwetsa mizinda yamalinga ndi kuisandutsa miyulu ya miyala. Anthu amene ankakhala kumeneko anali opanda mphamvu, ankada nkhaŵa, ndipo adaasokonezeka. Anali ngati mbeu zam'munda, ngati udzu wanthete. Anali ngati udzu wapadenga, umene mphepo imauumitsa usanakule nkomwe. “Koma Ine ndimadziŵa zonse za iwe, pamene ukhala pansi, pamene uyenda kwina ndi kubwerako, ndiponso pamene undikwiyira. Chifukwa chakuti udandikwiyira, ndipo kudzitukumula kwako kudamveka kwa Ine, ndidzakola mphuno yako ndi mbedza, ndi kuika chitsulo m'kamwa mwako. Ndidzakubweza pokuyendetsa m'njira yomwe udadzera pobwera.” Tsono Yesaya adauza mfumu Hezekiya kuti, “Chizindikiro cha zimene zidzachitika ndi ichi: Chaka chino mudzadya tirigu wa mphulumukwa. Chaka chamaŵa mudzadya tirigu wongodzimerera. Tsono chaka chamkucha mudzafesa tirigu nkukolola, mudzaoka mitengo yamphesa nkudya zipatso zake. Anthu a m'banja la Yuda amene adzatsalire adzapezanso bwino, ngati zomera zimene zazamitsa mizu pansi ndi kubala zipatso poyera. Ku Yerusalemu kudzafumira anthu otsala, ku phiri la Ziyoni kudzachokera gulu la anthu opulumuka. Changu cha Chauta chidzachitadi zimenezi. Zimene akunena Chauta za mfumu ya ku Asiriya ndi izi, akuti, ‘Sadzaloŵa mu mzinda umenewu, sadzaponyamo muvi ndi umodzi womwe. Ankhondo ake azishango sadzafika pafupi ndi mzinda umenewu, ndipo sadzauzinga ndi mtumbira wankhondo. Adzabwerera potsata njira yomwe adaadzera pobwera, ndipo sadzaloŵa mu mzinda umenewu. Ine Chauta ndatero. Ine ndidzautchinjiriza ndi kuuteteza mzinda umenewu chifukwa cha ulemerero wanga, ndiponso chifukwa cha chipangano changa chimene ndidachita ndi Davide mtumiki wanga.’ ” Ndiye usiku umenewo mngelo wa Chauta adapita ku zithando zankhondo za Aasiriya naphako asilikali 185,000. M'maŵa mwake adangoona asilikaliwo ali ngundangunda, atafa onsewo. Tsono Senakeribu, mfumu ya ku Asiriya, adachoka ndi kubwerera kwao, nakakhala ku Ninive. Tsiku lina pamene ankapembedza m'nyumba ya Nisiroki mulungu wake, ana ake aŵiri, Adrameleki ndi Sarezere, adamupha ndi malupanga ao, nathaŵira ku dziko la Ararati. Ndipo Esarahadoni, mwana wake wina, adaloŵa ufumu m'malo mwake. Nthaŵi imeneyo Hezekiya adaadwala, ndipo anali pafupi kufa. Mneneri Yesaya, mwana wa Amozi, adapita kukamuwona, namuuza kuti, “Chauta akuti ukonze zonse bwino lomwe, poti ufa, suchira ai.” Pomwepo Hezekiya adatembenuka nayang'ana ku khoma, nayamba kupemphera kwa Chauta kuti, “Inu Chauta, mukumbukire kuti ndakhala ndikukutumikirani mokhulupirika ndi modzipereka. Ndipo nthaŵi zonse ndinali kuchita zokukomerani.” Atatero adayamba kulira ndi mtima woŵaŵa. Tsono Yesaya asanatuluke m'bwalo lapakati, Chauta adamuuza kuti, “Bwerera, kamuuze Hezekiya, mfumu ya anthu anga, mau aŵa, ‘Ine Chauta, Mulungu wa Davide kholo lako, ndamva pemphero lako, ndipo misozi yako ndaiwona. Chabwino, ndidzakuchiritsa. Udzatha kukapembedza ku Nyumba ya Chauta mkucha. Ndipo ndidzakuwonjezera zaka khumi ndi zisanu pa moyo wako. Ndidzakupulumutsa iwe pamodzi ndi mzindawu kwa mfumu ya ku Asiriya. Mzindawu ndidzautchinjiriza chifukwa cha ulemu wanga ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.’ ” Pambuyo pake Yesaya adauza antchito a mfumu kuti, “Konzani phala lankhuyu. Kenaka mutengeko phalalo nkulimata pa chithupsa chake, kuti mfumu ichire.” Apo Hezekiya adafunsa Yesaya uja kuti, “Kodi padzakhala chizindikiro chanji choonetsa kuti Chauta adzandichiritsa, ndipo kuti ndidzatha kukapembedza ku Nyumba ya Chauta mkucha uno?” Yesaya adayankha kuti, “Chizindikiro chimene Chauta wakupatsa chakuti adzachitadi zimene adalonjeza nachi: Kodi chithunzithunzi chipite patsogolo kapena chibwerere pambuyo makwerero khumi?” Hezekiyayo adayankha kuti, “Nchapafupi kuti chithunzithunzi chipite patsogolo makwerero khumi, koma kuti chithunzithunzicho chibwerere m'mbuyo makwerero khumi, apo ndiponi.” Pamenepo mneneri Yesaya adatama Chauta mopemba. Ndipo Chauta adabweza chithunzithunzicho pambuyo makwerero khumi pa makwerero amene mfumu Ahazi adaamanga. Pa nthaŵi imeneyo Merodaki-Baladani, mwana wa Baladani, mfumu ya ku Babiloni, adatuma amithenga naŵapatsira makalata ndi mphatso, kuti akapereke kwa Hezekiya, poti adaamva kuti ankadwala. Hezekiya adaŵalandira anthuwo, naŵaonetsa nyumba yosungiramo zinthu zake, monga siliva, golide, zokometsera chakudya, mafuta onunkhira amtengowapatali, zida zonse zankhondo, ndiponso zonse zimene ankazisunga m'nyumba zake zosungiramo chuma. Panalibe kanthu kalikonse m'nyumbamo ndi mu ufumu wake wonse kamene sadaŵaonetse. Tsono mneneri Yesaya adapita kwa mfumu Hezekiya, namufunsa kuti, “Kodi anthu amene aja adakuuzani zotani, ndipo adaachokera kuti?” Hezekiya adayankha kuti, “Adaachokera ku dziko lakutali, ku Babiloni.” Yesaya adamufunsanso kuti, “Kodi m'nyumba mwanumo adaona chiyani?” Hezekiya adayankha kuti, “Adaona zonse za m'nyumba mwanga. Palibe ndi chinthu chimodzi chomwe chimene sindidaŵaonetse m'nyumba zanga zosungiramo chuma.” Pamenepo Yesaya adauza Hezekiya kuti, “Chauta akunena kuti nthaŵi idzafika pamene zonse za m'nyumba mwanu ndi zonse zimene makolo anu adazisonkhanitsa mpaka lero lino, adzakulandani kupita nazo ku Babiloni. Sipadzatsalapo ndi kanthu kamodzi komwe. Ambiri mwa ana anu, obala inu nomwe adzatengedwa, ndipo adzaŵasandutsa adindo ofulidwa otumikira ku nyumba ya mfumu ku Babiloni.” Tsono Hezekiya adauza Yesaya kuti, “Mau amene Chauta walankhulaŵa ngabwino.” Ponena zimenezo, Hezekiya ankaganiza kuti, “Palibe kanthu ai, malinga kuti padzakhale mtendere ndi bata masiku onse a moyo wanga.” Tsono ntchito zina za Hezekiya ndi mphamvu zake zonse ndi m'menenso adakumbira chidziŵe ndi ngalande zobwera ndi madzi mumzindamo, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda. Ndipo Hezekiya adamwalira naikidwa m'manda momwe adaikidwa makolo ake. Tsono Manase mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Manase anali wa zaka khumi ndi ziŵiri pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 55 ku Yerusalemu. Mai wake anali Hepeziba. Iyeyo adachita zoipa pamaso pa Chauta, potsata ntchito zonyansa za anthu a mitundu ina amene Chauta adaŵapirikitsa pofika Aisraele. Manaseyo adamanganso akachisi amene bambo wake Hezekiya adaaononga ku mapiri. Adamangira Baala maguwa, napanga mafano monga m'mene ankachitira Ahabu mfumu ya Aisraele. Ndipo ankapembedza zinthu zakuthambo namazitumikira. Adamangira mafanowo maguwa m'Nyumba ya Chauta imene Chautayo adaanena kuti, “Ku Yerusalemu ndiye kumene azikandipembedzerako.” Manase yemweyo adamangira zinthu zakuthambo maguwa m'mabwalo aŵiri a Nyumba ya Chauta. Pambuyo pake adapereka mwana wake wamwamuna ngati nsembe. Ankatama mizimu mopemba ndiponso ankaombeza maula, namachita zobwebwetetsa ndi zaufiti. Adachita zoipa zambiri zimene zidakwiyitsa Chauta. Adaika m'Nyumba ya Chauta fano losema la Asera. Nyumba imeneyo, Chauta anali atauza Davide ndi Solomoni mwana wake kuti, “M'nyumba iyi ndi mu Yerusalemu muno, ndimo m'mene ndasankha pakati pa mafuko onse a Israele kuti azindipembedzeramo mpaka muyaya. Tsono sindidzalola kuti Aisraele adzachotsedwe m'dziko lao limene ndidapatsa makolo ao, malinga kuti iwowo azisamala kuchita zinthu zonse motsata Malamulo amene ndaŵalamula, ndiponso motsata Malamulo amene Mose mtumiki wanga adaŵalamula.” Koma anthuwo sadamve zimenezo, ndipo Manase adaŵasokeretsa ndi kuŵachimwitsa kwambiri kupambana anthu a mitundu ina amene Chauta adaŵaononga pofika Aisraele. Nchifukwa chake Chauta adalankhula kudzera mwa atumiki ake aneneri, nati, “Manase mfumu ya ku Yuda wachita zonyansa zambiri, ndipo wachita zoipa kupambana zoipa zonse zimene ankachita Aamori amene adaalipo kale iye asanabadwe, ndipo wachimwitsanso anthu a ku Yuda ndi mafano akewo. Nchifukwa chake Ine Chauta, Mulungu wa Israele, ndikunena kuti, ‘Ndithu, ndidzabweretsa pa Yerusalemu ndi pa Yuda choipa chakuti aliyense amene adzachimve, adzadodoma nkupukusa mutu. Ndidzalanga Yerusalemu monga ndidalangira Samariya ndi Ahabu, pamodzi ndi banja lake. Tsono ndidzayeretsa Yerusalemu pochotsa anthu ake, monga momwe munthu amachitira popukuta mbale, ndipo ataipukuta amaivundikira pansi. Tsono anthu otsala ndidzaŵachotsa m'dziko ndi kuŵapereka m'manja mwa adani ao. Adzaphedwa ndipo adaniwo adzaŵalanda zonse. Zidzatero popeza kuti akhala akundichimwira ndipo andikwiyitsa, kuyambira tsiku limene makolo ao adatuluka ku Ejipito mpaka lero lino.’ ” Tsono Manase uja adakhetsa kwambiri magazi a anthu osachimwa, mpaka magaziwo kuyenderera m'miseu ya Yerusalemu kuyambira mbali ina mpaka mbali ina. Izi zidaonjezera pa machimo amene adachimwitsa nawo Ayuda pakuŵachititsa zoipa zonyoza Chauta. Tsono ntchito zina za Manase ndi zonse zimene adachita, ndiponso machimo amene adachita, zonsezo zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda. Choncho Manase adamwalira, naikidwa m'manda m'munda wa ku nyumba yake, m'munda wa Uza. Tsono Amoni mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Amoni anali wa zaka 22 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka ziŵiri ku Yerusalemu. Mai wake anali Mesulemeti, mwana wa Haruzi wa ku Yotiba. Iyeyo adachita zoipa pamaso pa Chauta monga m'mene ankachitira Manase bambo wake. Iyeyo ankatsata chitsanzo choipa cha bambo wake pazonse, namatumikira mafano amene bambo wake ankaŵatumikira ndi kumaŵapembedza. Adakana Chauta, Mulungu wa makolo ake, ndipo sadamvere malamulo ake. Tsono anyamata ake adamchita chiwembu, namupha m'nyumba mwake momwe. Koma anthu am'dzikomo adapha onse aja amene adamchita chiwembu mfumu Amoniyo. Kenanaka anthuwo adalonga Yosiya mwana wake kuti akhale mfumu m'malo mwake. Tsono ntchito zonse zimene adachita Amoni zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda. Atamwalira adaikidwa m'manda m'munda wa ku nyumba yake, m'munda wa Uza. Ndipo mwana wake Yosiya adaloŵa ufumu m'malo mwake. Yosiya anali wa zaka zisanu ndi zitatu pamene adadaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 31 ku Yerusalemu. Mai wake anali Yedida mwana wa Adaya wa ku Bozikati. Iyeyo adachita zolungama pamaso pa Chauta, namatsata chitsanzo cha Davide kholo lake pa zonse, osapatukira kumanja kapena kumanzere. Chaka cha 18 cha ufumu wake, Yosiya adatuma Safani mwana wa Azaliya, mwana wa Mesulamu, mlembi wa ku Nyumba ya Chauta, nati, “Pita kwa Hilikiya, mkulu wa ansembe, ukamuuze kuti aŵerenge ndalama zimene anthu abwera nazo ku Nyumba ya Chauta, zimene alonda apakhomo adasonkhanitsa kwa anthu. Ndalama zimenezo azipereke kwa akapitao okonzetsa Nyumba ya Chauta aja. Iwowo azipereke kwa antchito aja okonza Nyumba ya Chauta. Ndiye kuti alipire amisiri a matabwa, amisiri omanga nyumba, amisiri omanga ndi miyala ndiponso amene adapereka mitengo ndi miyala yosema yokonzera Nyumbayo. Koma anthu amene apatsidwe ndalama zolipirira antchito okonza Nyumbawo asaŵafunse kuti afotokoze za kamwazidwe ka ndalamazo, popeza kuti ndi anthu okhulupirika.” Tsono Hilikiya, mkulu wa nsembe uja, adauza Safani, mlembi uja, kuti, “Ndalipeza buku la Malamulo lija m'Nyumba ya Chauta.” Ndipo Hilikiya adapereka bukulo kwa Safani, iye naliŵerenga. Tsono Safani mlembi uja adapita kwa mfumu, nakafotokozera mfumuyo kuti, “Atumiki anu atenga ndalama zija zinali m'Nyumbazi, ndipo azipereka kwa anthu amene akuyang'anira ntchito yokonza Nyumba ya Mulungu.” Tsono Safani adauza mfumu kuti, “Wansembe Hilikiya wandipatsira buku.” Ndipo Safani adaliŵerenga bukulo pamaso pa mfumu. Mfumu itamva mau a m'buku la Malamulo, idang'amba zovala zake mwachisoni. Pomwepo idalamula wansembe Hilikiya, Ahikamu mwana wa Safani, Akibori mwana wa Mikaya, Safani mlembi uja ndi Asaya mtumiki wa mfumu, kuti, “Pitani mukafunse Chauta m'malo mwanga ndi m'malo mwa anthu a m'dziko lonse la Yuda, za mau a m'buku limene lapezekali. Ndithu mkwiyo wa Chauta umene watiyakirawu ngwaukulu, chifukwa choti makolo athu sadamvere mau a m'bukuli, ndipo sadatsate zonse zimene zidalembedwa m'menemo.” Motero wansembe Hilikiya, Ahikamu, Akibori, Safani ndi Asaya adapita kwa mneneri wamkazi dzina lake Hulida, mkazi wa Salumu. Salumuyo, wosunga zovala zachifumu anali mwana wa Tikiwa, mwana wa Harihasi. Mkaziyu ankakhala ku Yerusalemu m'dera latsopano la mzindawo. Tsono anthu aja atalankhula naye, iyeyo adaŵauza kuti, “Chauta, Mulungu wa Israele, akunena kuti, ‘Muuzeni munthu wakutumani kwa Ineyo kuti, Ine Chauta ndikuti, Ndidzabweretsa choipa pa mzinda uno ndi pa anthu onse am'menemo, potsata mau onse a m'buku limene mfumu ya ku Yuda idaliŵerenga. Chifukwa chakuti anthuwo andisiya Ine namafukiza lubani kwa milungu ina, nkumandichimwira ndi mafano ao, ntchito zonse za manja ao, Ine pano mkwiyo wanga wayakira mzinda uno ndipo sudzazima. Koma mfumu ya ku Yuda imene idakutumani kuti mukafunse Chauta, mukaiwuze kuti Ine Chauta Mulungu wa Aisraele ndikuti, Kumva wamvadi mauwo, pakuti mtima wako walapa ndipo wadzichepetsa pamaso pa Ine Chauta, utamva mau amene ndidalankhula otsutsa mzinda uno ndi anthu onse okhala m'menemo. Ndithudi mzinda uno udzakhala bwinja ndi malo otembereredwa. Popeza kuti wang'amba zovala zako numalira pamaso panga, Inenso ndamva pemphero lako, ndatero Ine Chauta. Nchifukwa chake Ine ndidzakutenga, iweyo ukalondole makolo ako ndipo udzaikidwa m'manda mwamtendere. Motero maso ako sadzaona zoipa zija zimene ndidzabweretsa pa mzinda uno.’ ” Tsono anthu aja adabwerera nakanena mau amenewo kwa mfumu. Pamenepo mfumu Yosiya adatumiza mau kukaitana akuluakulu onse a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti adzasonkhane. Ndipo mfumuyo idapita ku Nyumba ya Chauta pamodzi ndi anthu onse a ku Yuda, nzika zonse za mu Yerusalemu, ansembe ndi aneneri, ndiponso anthu onse aakulu ndi aang'ono omwe. Tsono iye adaŵerenga pamaso pao mau onse a m'buku lija la chipangano limene lidaapezeka m'Nyumba ya Mulungu. Kenaka mfumuyo idaimirira pa nsanja yake, ndipo idachita chipangano pamaso pa Chauta kuti idzatsata njira za Chauta, ndipo kuti idzasunga mau, malamulo ndi malangizo ake ndi mtima wake wonse ndiponso ndi moyo wake wonse, ndipo kuti idzagwiritsa ntchito mau a chipangano chimenechi monga momwe adalembedwera m'bukulo. Tsono anthu onse nawonso adavomera kutsata chipanganocho. Tsono mfumu Yosiya adalamula Hilikiya, wansembe wamkulu, ndiponso ansembe othandiza ndi alonda apakhomo, kuti achotse m'Nyumba ya Mulungu zinthu zonse zopembedzera Baala, fano la Asera ndiponso mafano a zinthu zakuthambo. Zonsezo adazitenthera kunja kwa Yerusalemu, ku minda ya ku Kidroni, ndipo phulusa lake adapita nalo ku Betele. Yosiya adatulutsa ansembe a mafano amene mafumu a ku Yuda adaŵakhazika kuti azipereka nsembe ku akachisi ku mizinda ya m'dziko la Yuda ndi ku malo ozungulira Yerusalemu. Adatulutsanso amene ankapereka nsembe kwa Baala, kwa dzuŵa, kwa mwezi, kwa nyenyezi ndi kwa zinthu zonse zakuthambo. Adachotsa fano la Asera m'Nyumba ya Chauta, napita nalo kunja kwa Yerusalemu ku mtsinje wa Kidroni. Tsono adalitenthera ku mtsinje wa Kidroniko, naliperapera, nkutaya phulusa lake pa manda a anthu wamba. Adagwetsa tinyumba ta amuna ochitana zadama ku Nyumba ya Mulungu, ku malo amene akazi ankalukira mikanjo yovala anthu opembedza Asera. Yosiya adabwera nawo ansembe a ku mizinda ya ku Yuda, naononga akachisi opembedzerako mafano kumene ansembe aja ankaperekera nsembe, kuyambira ku Geba mpaka ku Beereseba. Adagwetsa akachisi onse amene anali pa chipata cha khomo la Yoswa, nduna ya mzindawo. Maloŵa anali ku dzanja lamanzere la khomo la mzindawo. Ansembe a ku akachisiwo sadaŵalole kufika ku guwa la Chauta ku Yerusalemu, komabe ankadya nao buledi wosatupitsa ndi ansembe anzao kumeneko. Mfumu Yosiya adaononganso ng'anjo yotchedwa Tofeti imene inali m'chigwa cha ana a Hinomu, kuti munthu aliyense asapereke mwana wake wamwamuna kapena wamkazi ngati nsembe kwa Moleki. Adachotsanso akavalo amene mafumu a ku Yuda adaaŵapereka ngati nsembe kwa dzuŵa. Akavalo amenewo ankaŵasunga pa bwalo la Nyumba ya Mulungu pafupi ndi chipata choloŵera m'Nyumbamo, ndiponso chipinda cha Natani Meleki, mkulu wosunga nyumbayo. Kenaka adatentha magaleta opembedzera dzuŵa. Pambuyo pake mfumuyo idagwetsa ndi kuphwanyaphwanya maguwa a pa denga la chipinda chapamwamba cha Ahazi, amene adaŵamanga mafumu a ku Yuda, ndiponso maguwa amene Manase adaŵamanga pa mabwalo aŵiri a Nyumba ya Chauta. Ndipo adataya fumbi lake mu mtsinje wa Kidroni. Pambuyo pake mfumuyo idaononganso akachisi opembedzerapo mafano amene anali kuvuma kwa Yerusalemu, kumwera kwa phiri lotchedwa Chiwonongeko. Maguwawo Solomoni, mfumu ya ku Israele, adaaŵamangira fano lonyansa la Asidoni lotchedwa Asitoreti, ndi la Amowabu lotchedwa Kemosi, ndiponso la Aamoni lotchedwa Milikomu. Adaphwanyanso zipilala zamiyala naononga mafano onse a Asera, ndipo pa malo ao adamwazapo mafupa a anthu akufa. Yosiya adagwetsanso guwa la ku Betele, limene Yerobowamu, mwana wa Nabati, adaalimanga ku kachisi pa chitunda. Yerobowamuyo adaachimwitsa Aisraele ndi guwa limenelo. Ndipo Yosiya adagumula guwalo naphwanyanso miyala yake, nkuiperapera, naisandutsa fumbi. Adatenthanso kachisiyo, pamodzi ndi mafano a Asera. Atatero, Yosiya adacheuka naona manda paphiripo. Tsono adatuma anthu kuti akatenge mafupa m'mandamo, ndipo adaŵatenthera paguwapo. Potero adalidetsa monga momwe Chauta adaanenera kudzera mwa mneneri wake amene adaaloseratu zimenezi. Apo mfumu idafunsa kuti, “Kodi manda ena ndikuwona apowo ngayani?” Anthu amumzindamo adamuuza kuti, “Amenewo ndi manda a mneneri wa Mulungu wa ku Yuda amene adaneneratu za zimene inu mwalichita guwa la ku Betele.” Yosiya adati, “Mlekeni. Munthu asachotse mafupa akewo ai.” Motero mafupawo adangoŵaleka pamodzi ndi mafupa a mneneri wa ku Samariya uja. Yosiyayo adaononganso nyumba zonse zopembedzeramo mafano zija zimene zinali m'mizinda ya ku Samariya. Mafumu a ku Israele ndiwo amene adaamanga zimenezi, naputa mkwiyo wa Chauta potero. Yosiya uja adachita chimodzimodzi kumeneko monga momwe adaachitira ku Betele. Adapha ansembe onse amene ankatumikira ku nyumba zochipembedzeramo mafano kumeneko. Adaŵaphera pa maguwa ao, natentha mafupa a anthuwo pamaguwapo. Pambuyo pake adabwerera ku Yerusalemu. Tsono mfumu Yosiya adalamula anthu onse kuti, “Muchite chikondwerero cha Paska, kulemekeza Chauta, Mulungu wanu, potsata zimene zidalembedwa m'buku lachipangano.” Paska yotereyi inali isanachitikepo kuyambira nthaŵi ya aweruzi amene ankatsogolera Aisraele, kapena nthaŵi ya mafumu a ku Israele, kapenanso nthaŵi ya mafumu a ku Yuda. Koma chaka cha 18 cha ufumu wa Yosiya, Paska imeneyi adaichitira Chauta ku Yerusalemu. Masiku amenewo Yosiya adachotsanso anthu amaula, amatsenga, milungu ya m'nyumba ndiponso mafano ena onse, kudzanso zonyansa zonse zimene zinali ku dziko la Yuda ndi ku Yerusalemu. Adachita zimenezi kuti atsate Malamulo amene adalembedwa m'buku lomwe wansembe Hilikiya adalipeza m'Nyumba ya Chauta. Yosiyayo asanaloŵe ufumu, panalibenso mfumu ina yofanafana naye imene idatembenukira kwa Chauta ndi mtima wake wonse, ndi moyo wake wonse ndiponso ndi mphamvu zake zonse, potsata Malamulo a Mose. Ndipo iye atafa, sipadakhalenso wina aliyense wofanafana ndi iyeyo. Komabe Chauta sadaleke kukwiya kwake koopsa kumene adakwiyira Yuda, chifukwa choti Manase adaachita kuuputa mkwiyo wa Chautawo. Choncho Chauta adati, “Ngakhale anthu a ku Yuda omwe, ndidzaŵachotsa pamaso panga, monga momwe ndachotsera anthu a ku Israele. Ndidzagwetsa ngakhale mzinda uno wa Yerusalemu umene ndidausankha, pamodzi ndi Nyumba imene ndidati, ‘Dzina langa lidzakhala m'menemo.’ ” Tsono ntchito zina za Yosiya pamodzi ndi zonse zimene adazichita zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda. Pa masiku akewo Farao Neko, mfumu ya ku Ejipito, adapita kukathandiza mfumu ya ku Asiriya ku mtsinje wa Yufurate. Mfumu Yosiya adapita kukamenyana naye nkhondo. Koma Farao Neko adamupha Yosiyayo ku Megido pa nkhondoyo. Pamenepo nduna zake zidamnyamulira pa galeta kuchokera ku Medigo, nkupita naye ku Yerusalemu, ndipo zidamuika m'manda akeake. Kenaka anthu a ku Yuda adatenga Yehowahazi mwana wa Yosiya namdzoza, ndipo iyeyo adaloŵa ufumu m'malo mwa bambo wake. Yehowahazi anali wa zaka 23 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira miyezi itatu ku Yerusalemu. Mai wake anali Hamutala, mwana wa Yeremiya wa ku Libina. Adachita zoipa kuchimwira Chauta potsata zonse zimene makolo ake ena ankachita. Tsono Farao Neko adamuika m'ndende ku Ribula m'dziko la Hamati, kuti asalamulirenso ku Yerusalemu. Pambuyo pake Faraoyo adaŵakhometsa msonkho wa siliva wolemera makilogramu 3,400, ndiponso golide wolemera makilogramu 34. Kenaka Farao Neko wa ku Ejipito adaika Eliyakimu, mwana wa Yosiya, kuti akhale mfumu m'malo mwa bambo wake, ndipo adasintha dzina lake kuti akhale Yehoyakimu. Farao Neko adatenga Yehowahazi kupita naye ku Ejipito, ndipo adafera komweko. Tsono Yehoyakimu nayenso ankapereka siliva ndi golide kwa Farao. Komatu ankachita kukhometsa msonkho m'dziko mwakemo kuti apereke ndalamazo kwa Farao, monga momwe Farao adamlamulira. Ankatenga siliva amene anthu am'dzikomo ankayenera kukhoma, pamodzi ndi golide yemwe, malinga ndi chuma cha munthu aliyense, ndipo ankazipereka kwa Farao Neko. Yehoyakimu anali wa zaka 25 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka khumi ndi chimodzi ku Yerusalemu. Mai wake anali Zebida, mwana wa Pedaya, wa ku Ruma. Yehoyakimu adachita zoipa kuchimwira Chauta potsata zonse zimene makolo ake ena ankachita. Pa nthaŵi ya Yehoyakimu, Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adadzathira nkhondo dziko la Yuda, ndipo Yehoyakimu adakakamizidwa kutumikira Nebukadinezarayo zaka zitatu. Koma pambuyo pake Yehoyakimuyo adapandukira Nebukadinezara. Tsono Chauta adatumiza magulu ankhondo a Ababiloni, a Asiriya, a Amowabu, ndi a Aamoni kuti akathire nkhondo Yuda, mpaka kuwononga dzikolo, monga momwe Chauta adaanenera kudzera mwa atumiki ake aneneri. Zoonadi, zimenezi zidagwera Yuda, monga momwe Chauta adaalamulira. Adachotsa Ayudawo pamaso pake, chifukwa cha zoipa zimene mfumu Manase ankachita, ndiponso chifukwa cha magazi a anthu osachimwa amene iye adakhetsa. Manaseyu adadzaza Yerusalemu ndi magazi a anthu osachimwa, ndipo Chauta sadamkhululukire ai. Tsono ntchito zina za Yehoyakimu ndi zonse zimene adazichita zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda. Motero Yehoyakimu adamwalira, naikidwa m'manda. Ndipo Yehoyakini mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Nthaŵi imeneyo mfumu ya ku Ejipito sidatulukenso m'dziko lake, poti mfumu ya ku Babiloni inali italanda maiko onse a mfumu ya ku Ejipito kuchokera ku mtsinje wa ku Ejipito mpaka ku mtsinje wa Yufurate. Yehoyakini anali wa zaka 18 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira miyezi itatu ku Yerusalemu. Mai wake anali Nehusita, mwana wa Elinati, wa ku Yerusalemu. Yehoyakini adachita zoipa pamaso pa Chauta potsata zonse zimene ankachita bambo wake. Nthaŵi imeneyo ankhondo a Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, adadza ku Yerusalemu, nazinga mzindawo ndi zithando zankhondo. Ndipo Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adafika ku mzindawo pa nthaŵi imene ankhondo ake ankauzinga. Tsono Yehoyakini mfumu ya ku Yuda adadzipereka kwa mfumu ya ku Babiloni, pamodzi ndi mai wake, alangizi ake, nduna zake ndiponso akuluakulu a kunyumba kwake. Mfumu ya ku Babiloni idamgwira Yehoyakini ukapolo pa chaka chachisanu ndi chitatu cha ufumu wake. Adatenga chuma chonse cha ku Nyumba ya Chauta, pamodzi ndi chuma chonse cha ku nyumba ya mfumu. Adaononga ziŵiya zonse zagolide za ku Nyumba ya Chauta zimene Solomoni mfumu ya ku Israele adapanga. Adatenga anthu onse a ku Yerusalemu, ndiye kuti nduna zonse ndi anthu onse amphamvu. Onsewo pamodzi analipo 10,000. Adatenganso anthu onse aluso ndi amisiri osula. Sadatsalepo ndi mmodzi yemwe, kupatula anthu osauka okha am'dzikomo. Nayenso Yehoyakini adamtenga kupita naye ku Babiloni. Adatenganso mai wake wa mfumuyo, akazi ake, nduna zake ndiponso anthu omveka am'dzikomo. Onsewo adaŵagwira ukapolo ku Yerusalemu kunka nawo ku Babiloni. Tsono mfumu ya ku Babiloni idagwira ukapolo anthu otchuka onse okwanira 7,000, ndiponso anthu aluso pamodzi ndi amisiri osula 1,000. Onsewo anali amphamvu odziŵa kumenya nkhondo. Kenaka mfumu ya ku Babiloni idalonga ufumu Mataniya, malume wa Yehoyakini, m'malo mwake, ndipo adasintha dzina lake kuti akhale Zedekiya. Zedekiya anali wa zaka 21 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka khumi ndi chimodzi ku Yerusalemu. Mai wake anali Hamutala, mwana wa Yeremiya, wa ku Libina. Zedekiyayo adachita zoipa pamaso pa Chauta potsata zonse zimene ankachita Yehoyakimu. Chifukwa cha zonse zimene zidachitika ku Yerusalemu ndi ku Yudazi, Chauta adakwiya kwambiri, mpaka kuŵachotsa anthuwo pamaso pake. Tsono Zedekiya adapandukira mfumu ya ku Babiloni. Ndiye pa chaka chachisanu ndi chinai cha ufumu wa Zedekiyayo, mwezi wakhumi, pa tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adabwera ndi ankhondo ake onse, kudzathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu. Adauzinga ndi zithando zankhondo ponseponse. Motero mzindawo udaazingidwa ndi zithandozo mpaka chaka cha 11 cha ufumu wa Zedekiya. Tsono pa tsiku lachisanu ndi chinai pa mwezi wachinai chaka chimenecho, pamene njala inali itakula kwambiri mumzindamo, kotero kuti anthu analibiretu chakudya m'dzikomo, malinga a mzindawo adabooledwa. Pamenepo mfumu Zedekiya adathaŵa usiku pamodzi ndi ankhondo ake onse kutulukira pa chipata cha pakati pa makoma aŵiri, pafupi ndi munda wa mfumu, ngakhale kuti Ababiloni anali atauzinga mzinda wonsewo. Ndipo adaloŵera cha ku Araba. Koma gulu lankhondo la ku Babiloni lidamlondola mfumu Zedekiya nkukamgwirira m'zigwa za ku Yeriko. Ankhondo ake adabalalika namsiya. Apo a ku Babiloni aja atamgwira Zedekiyayo, adapita naye kwa Nebukadinezara, ku Ribula. Komweko Nebukadinezarayo adagamula mlandu wa Zedekiya uja. Pompo adapha ana a Zedekiya iyeyo akupenya, ndipo adamkolowola maso Zedekiyayo, nammanga ndi maunyolo, nkupita naye ku Babiloni. Mwezi wachisanu, pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri la mwezi, chaka cha 19 cha ufumu wa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, Nebuzaradani, mkulu wa asilikali oteteza mfumu, mmodzi mwa alangizi ake, adadza ku Yerusalemu. Ndipo adatentha Nyumba ya Chauta, nyumba ya mfumu, ndi nyumba zina zonse za ku Yerusalemu. Adatentha nyumba yaikulu iliyonse. Tsono gulu lonse lankhondo la ku Babiloni limene linali ndi mkulu wa asilikali uja, lidagumula malinga ozinga Yerusalemu. Anthu ena onse amene adaatsala mumzindamo, ndi ena amene adaathaŵa kupita kwa mfumu ya ku Babiloni, pamodzi ndi ena otsala, Nebuzaradani, mkulu wa asilikali uja, adaŵatenga kupita nawo ku Babiloni. Koma mkulu wa asilikaliyo adasiyako anthu ena osauka kwambiri am'dzikomo, kuti azisamala minda yamphesa ndi minda ina. Ankhondo a ku Babiloni adaphwanya nsanamira zamkuŵa za m'Nyumba ya Chauta ndiponso maphaka ndi chimbiya chamkuŵa, ndipo adatenga mkuŵawo, napita nawo ku Babiloni. Ankhondowo adachotsanso mbiya, zoolera phulusa, zozimira nyale, mbale zofukizira lubani kudzanso ziŵiya zonse zamkuŵa zimene ankagwiritsira ntchito ku Nyumba ya Chauta. Mkulu wa asilikali uja adatenganso ziwaya zosonkhapo moto ndiponso mbale zowazira madzi, ndi zina zonse zagolide ndi zasiliva. Kunena za nsanamira ziŵiri zija, chimbiya, ndi maphaka zimene Solomoni adaapangira Nyumba ya Chauta, kulemera kwake kwa mkuŵa wa zonsezo kunali kosaŵerengeka. Msinkhu wa nsanamira imodzi unali mamita asanu ndi atatu, ndipo pamwamba pake panali mutu wamkuŵa. Msinkhu wa mutuwo unali mita imodzi ndi theka. Ukonde wake pamodzi ndi makangaza ake, zonsezo zinali zamkuŵa, ndipo zinali pamwamba pa mutu uja mozungulira. Nsanamira yachiŵiri inali yolingana ndi inayo, ndipo inalinso ndi ukonde. Tsono mkulu wa asilikali uja adagwira Seraya mkulu wa nsembe ndi Zefaniya wachiŵiri kwa mkulu wa ansembe, ndi alonda atatu apakhomo. Mumzindamo adagwiramo mkulu amene ankalamulira ankhondo ndiponso anthu asanu amene anali aphungu a mfumu mumzindamo. Adagwiranso mlembi wa mtsogoleri wa ankhondo amene ankapemba anthu am'dzikomo ndiponso akuluakulu ena 60, amene anali mumzindamo. Nebuzaradani, mkulu wa asilikali uja, adaŵatenga onsewo napita nawo kwa mfumu ya ku Babiloni ku Ribula. Ndipo mfumuyo idalamula kuti aŵakwapule ndi kuŵaphera ku Ribula, m'dziko la Hamati. Umu ndimo m'mene Ayuda adatengedwera ukapolo kuŵachotsa ku dziko lao. Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adaika Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, kuti akhale kazembe woyang'anira anthu otsala aja amene Nebukadinezarayo adaŵasiya ku dziko la Yuda. Tsono atsogoleri Achiyuda ndi ankhondo ao onse amene anali atathaŵa, atamva kuti mfumu ya ku Babiloni idaika Gedaliya kuti akhale kazembe, adadza kwa Gedaliya ku Mizipa, iwo pamodzi ndi anthu ao. Atsogoleriwo maina ao anali aŵa: Ismaele mwana wa Netaniya, Yohanani mwana wa Kareya, Seraya mwana wa Tanihumeti wa ku Netofa ndi Yazaniya mwana wa Maakati. Iwowo pamodzi ndi anthu ao, Gedaliya adaŵalonjeza molumbira kuti, “Musaope chifukwa cha atsogoleri a Ababiloniwo. Khalani m'dzikomu, muzimvera mfumu ya ku Babiloni, ndipo zinthu zidzakuyenderani bwino.” Koma pa mwezi wa chisanu ndi chiŵiri Ismaele mwana wa Netaniya, mwana wa Elisama, wa banja laufumu, adadza pamodzi ndi anthu khumi. Adadzathira nkhondo Gedaliya, napha iyeyo ndiponso Ayuda ndi anthu a ku Babiloni amene anali naye limodzi ku Mizipa. Pamenepo Aisraele onse, olemera ndi osauka omwe, pamodzi ndi atsogoleri ankhondo, adanyamuka kupita ku Ejipito, poti ankaopa Ababiloni. Pa chaka cha 37 cha kutengedwa ukapolo Yehoyakini mfumu ya ku Yuda, pa mwezi wa 12 pa tsiku la 27 la mwezi, Evili-Merodaki mfumu ya ku Babiloni, pa chaka choyamba cha ufumu wake, adakomera mtima Yehoyakiniyo nammasula m'ndende. Adamchitira zabwino, namkweza kupambana mafumu ena onse amene anali naye limodzi ku Babiloni. Motero Yehoyakini adaloledwa kuchotsa zovala zakundende, ndi kumadya ku tebulo la mfumu masiku onse a moyo wake. Mfumuyo inkampatsa phoso tsiku lililonse pa moyo wake wonse. Adamu adabereka Seti, Seti adabereka Enosi, Enosi adabereka Kenani, Kenani adabereka Mahalalele, Mahalalele adabereka Yaredi, Yaredi adabereka Enoki, Enoki adabereka Metusela, Metusela adabereka Lameki, Lameki adabereka Nowa, Nowa adabereka Semu, Hamu ndi Yafeti. Ana a Yafeti naŵa: Gomeri, Magogi, Madai, Yavani, Tubala, Meseki ndi Tirasi. Ana a Gomeri naŵa: Asikenazi, Rifati ndi Togarima. Ana a Yavani naŵa: Elisa, Tarisisi, Kitimu ndi Rodanimu. Ana a Hamu naŵa: Kusi, Ejipito, Puti ndi Kanani. Ana a Kusi naŵa: Seba, Havila, Sabita, Raama ndi Sabiteka. Ana a Raama naŵa: Sheba ndi Dedani. Kusi adabereka Nimirodi. Iyeyu ndiye adayamba kukhala munthu wamphamvu pa dziko lonse lapansi. Ejipito adabereka Ludimu, Anamimu, Lehabimu, Nafituhimu, Patirusimu, Kasiluhimu (kholo la Afilisti) ndi Kafitorimu. Kanani adabereka Sidoni mwana wake wachisamba ndi Heti. Kanani analinso kholo la Ayebusi, Aamori, Agirigasi, Ahivi, Aariki, Asini, Arivadi, Azemari ndi Ahamati. Ana a Semu naŵa: Elamu, Asuri, Aripakisadi, Ludi, Aramu, Uzi, Huli, Getere ndi Meseki. Aripakisadi adabereka Sela. Sela adabereka Ebere. Ebere adabereka ana aamuna aŵiri. Mwana wina anali Pelegi (pakuti anthu adaagaŵikana pa nthaŵi yake), ndipo mbale wake anali Yokotani. Yokotani adabereka Alimodadi, Selefi, Hazara-Maveti, Yera, Hadoramu, Uzali, Dikila, Ebala, Abimaele, Sheba, Ofiri, Havila ndi Yobabu. Onseŵa anali ana a Yokotani. A m'banja la Semu anali aŵa: Aripakisadi, Sela, Ebere, Pelegi, Reu, Serugi, Nahori, Tera, ndi Abramu, ndiye kuti Abrahamu. Ana a Abrahamu naŵa: Isaki ndi Ismaele. Mibadwo yao nayi: mwana wachisamba wa Ismaele anali Nebayoti. Panalinso Kedara, Adibeele, Mibisamu, Misima, Duma, Masa, Hadadi, Tema, Yeturi, Nafisi ndi Kedema. Ana a Ketura mzikazi wa Abrahamu naŵa: Zimirani, Yokosamu, Medani, Midiyani, Isibaki, ndiponso Suwa. Ana a Yokosamu naŵa: Sheba ndi Dedani. Ana a Midiyani naŵa: Efa, Efere, Hanoki, Abida ndi Elida. Onseŵa anali zidzukulu za Ketura. Abrahamu adabereka Isaki. Ana a Isaki naŵa: Esau ndi Israele. Ana a Esau naŵa: Elifazi, Reuele, Yeusi, Yalamu ndi Kora. Ana a Elifazi naŵa: Temani, Omara, Zefi, Gatamu, Kenazi, Timna ndi Amaleke. Ana a Reuele naŵa: Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Ana a Seiri naŵa: Lotani, Sobala, Zibiyoni, Ana, Disoni, Ezere ndi Disani. Ana a Lotani naŵa: Hori ndi Honamu. Mlongo wake wa Lotani anali Timna. Ana a Sobala naŵa: Aliyani, Manahati, Ebala, Sefi ndi Onamu. Ana a Zibiyoni naŵa: Aiya ndi Ana. Mwana wa Ana anali Disoni. Ana a Disoni naŵa: Hamurani, Esibani, Itirani, ndi Kerani. Ana a Ezere naŵa: Bilihani, Zaavani ndi Yaakani. Ana a Disani naŵa: Uzi ndi Arani. Naŵa mafumu amene ankalamulira ku dziko la Edomu, Aisraele adakalibe mfumu iliyonse: Bela mwana wa Beori, ndipo mzinda wake unali Dinaba. Bela atafa, Yobabu mwana wa Zera wa ku Bozira, adaloŵa ufumu m'malo mwake. Yobabu atafa, Husamu wa ku dziko la Temani adaloŵa ufumu m'malo mwake. Husamu atafa, Hadadi mwana wa Bedadi, amene adagonjetsa Amidiyani ku dziko la Mowabu, adaloŵa ufumu m'malo mwake. Mzinda wake ankautchula kuti Aviti. Hadadi atafa, Samila wa ku Masireka adaloŵa ufumu m'malo mwake. Samila atafa, Shaulo wa ku Rehoboti ku Yufurate, adaloŵa ufumu m'malo mwake. Shaulo atafa, Baala-Hanani mwana wa Akibori adaloŵa ufumu m'malo mwake. Baala-Hanani atafa, Hadadi adaloŵa ufumu m'malo mwake. Mzinda wake ankautchula kuti Pai. Mkazi wake anali Metabele mwana wa Materedi, mwana wa Mezahabu. Hadadi nayenso nkufa. Mafumu a ku Edomu anali aŵa: Timna, Aliva, Yeteti, Oholibama, Ela, Pinoni, Kenazi, Temani, Mibizara, Magadiele ndi Iramu. Ameneŵa ndiwo mafumu a ku Edomu. Ana a Israele naŵa: Rubeni, Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, Zebuloni, Dani, Yosefe, Benjamini, Nafutali, Gadi, ndi Asere. Ana a Yuda naŵa: Eri, Onani, ndi Sela. Ana atatu ameneŵa adamubalira ndi Batisuwa mkazi wa ku Kanani. Tsono Eri mwana wa Yuda anali wa makhalidwe oipa, choncho Chauta adamupha. Mpongozi wake Tamara nayenso adamubalira Perezi ndi Zera. Ana onse a Yuda analipo asanu. Ana a Perezi naŵa: Hezironi ndi Hamuli. Ana a Zera naŵa: Zimiri, Etani, Hemani, Kalikoli ndi Dara. Onse pamodzi analipo asanu. Ana a Karimi naŵa: Akara amene adaavuta Aisraele. Iyeyo adaaba zinthu zoyenera kuziwononga. Mwana wa Etani anali Azariya. Ana amene adabereka Hezironi naŵa: Yerameele, Ramu ndi Kelebe. Ramu adabereka Aminadabu, Aminadabu adabereka Nasoni, mkulu wa fuko la Yuda. Nasoni adabereka Salimoni, Salimoni adabereka Bowazi, Bowazi adabereka Obede, Obede adabereka Yese. Yese adabereka Eliyabu mwana wake wachisamba, wachiŵiri Abinadabu, wachitatu Simea, wachinai Netanele, wachisanu Radai, wachisanu ndi chimodzi Ozemu, wachisanu ndi chiŵiri Davide. Alongo ao anali Zeruya ndi Abigaile. Ana a Zeruya naŵa: Abisai, Yowabu ndi Asahele, onse pamodzi atatu. Abigaile adabala Amasa ndipo bambo wake wa Amasa anali Yetere Mwismaele. Kalebe mwana wa Hezironi anali nawo ana omubalira mkazi wake Azuba ndiponso Yerioti. Ana amene adabala mkaziyo naŵa: Yesere, Sobabu ndi Aridoni. Atafa Azuba, Kalebe adakwatira Efrati amene adamubalira Huri. Huri adabereka Uri, ndipo Uri adabereka Bezalele. Pambuyo pake Hezironi, ali wa zaka 60, adakakwatira mwana wa Makiri bambo wake wa Giliyadi. Ndipo mkaziyo adamubalira Segubu. Segubu adabereka Yairi amene anali ndi mizinda 23 m'dziko la Giliyadi. Koma anthu a ku Gesuri ndi a ku Aramu adaŵalanda Havoti-Yairi, Kenati pamodzi ndi midzi yake yomwe, yonse pamodzi inalipo midzi 60. Onseŵa anali adzukulu a Makiri, bambo wake wa Giliyadi. Atafa Hezironi, Kalebe adakwatira Efurata, mkazi wa bambo wake Hezironi. Ndipo mkaziyo adamubalira Asuri, bambo wake wa Tekowa. Ana a Yerameele, mwana wachisamba wa Hezironi, naŵa: Ramu mwana wachisamba, Buna, Oreni, Ozemu, ndi Ahiya. Yerameele analinso ndi mkazi wina dzina lake Atara. Mkaziyu adabala Onamu. Ana a Ramu, mwana wachisamba wa Yerameele, anali Maazi, Yamini ndi Ekeri. Ana a Onamu anali Samai ndi Yada. Ana a Samai anali Nadabu ndi Abisuri. Mkazi wake wa Abisuri anali Abihaili, ndipo mkaziyo adamubalira Abani ndi Molidi. Ana a Nadabu anali Seledi ndi Apaimu. Seledi adafa opanda ana. Mwana wa Apaimu anali Isi. Mwana wa Isi anali Sesani. Mwana wa Sesani anali Alai. Ana a Yada mbale wa Samai anali Yetere ndi Yonatani. Yetere adafa opanda ana. Ana a Yonatani anali Peleti ndi Zaza. Ameneŵa ndiwo amene anali zidzukulu za Yerameele. Sesani analibe ana aamuna, anali ndi ana aakazi okhaokha. Koma anali ndi kapolo wake wa ku Ejipito, dzina lake Yara. Motero Sesani adakwatitsa mwana wake wamkazi kwa Yara kapolo wake uja. Ndipo mkaziyo adamubalira Attai. Attai adabereka Natani, Natani adabereka Zabadi. Zabadi adabereka Efilala, Efilala adabereka Obede. Obede adabereka Yehu, Yehu adabereka Azariya. Azariya adabereka Helezi, Helezi adabereka Eleasa. Eleasa adabereka Sisimai, Sisimai adabereka Salumu. Salumu adabereka Yekamiya, ndipo Yekamiya adabereka Elisama. Ana a Kalebe mbale wa Yerameele naŵa: Maresa, mwana wake wachisamba, bambo wake wa Zifi. Mwana wa Maresa anali Hebroni. Ana a Hebroni naŵa: Kora, Tapuwa, Rekemu ndi Sema. Sema adabereka Rahama, bambo wake wa Yorikeamu ndipo Rekemu adabereka Samai. Mwana wa Samai anali Maoni. Tsono Maoni adabereka Betezuri. Nayenso Efa, mzikazi wa Kalebe, adamubalira Harani, Moza ndi Gazezi. Harani adabereka Gazezi. Ana a Yadai naŵa: Regemu, Yotamu, Gesani, Peleti, Efa ndi Saafi. Maaka, mzikazi wa Kalebe, adamubalira Sebere ndi Tirihana. Mkaziyo adabalanso Saafi, bambo wake wa Madimana, ndi Seva bambo wake wa Makibena ndiponso bambo wa Gibea. Mwana wamkazi wa Kalebe anali Akisa. Ameneŵa ndiwo amene anali zidzukulu za Kalebe. Ana a Huri, mwana wachisamba wa Efurata, naŵa: Sobala amene adabereka Kiriyati-Yearimu, Salima amene adabereka Betelehemu, ndiponso Harefi amene adabereka Betegadere. Sobala bambo wake wa Kiriyati-Yearimu adaberekanso ana ena, naŵa: Harowe, ndiye kuti theka la Amenuwoti. Mabanja a Kiriyati-Yearimu naŵa: Aitiri, Aputi, Asumati ndi Amisirai. Ameneŵa ndiwo makolo a Azorati ndi Aesitaoli. Ana a Salima naŵa: Betelehemu, Anetofa, Ataroti-Beti-Yowabu ndi hafu la Amanahati, ndiponso Azori. Mabanjanso a alembi amene ankakhala ku Yabesi naŵa: Atirati, Asimeati ndi Asukati. Ameneŵa ndiwo Akeni amene adachokera kwa Hamati, kholo la banja la Rekabu. Naŵa ana a Davide amene adabadwira ku Hebroni. Amoni ndiye mwana wake wachisamba, mai wake anali Ahinowamu, wa ku Yezireele. Daniele ndiye mwana wake wachiŵiri, mai wake anali Abigaile, wa ku Karimele. Mwana wake wachitatu ndi Abisalomu, mai wake anali Maaka, mwana wa Talimai, mfumu ya ku Gesuri. Mwana wake wachinai ndi Adoniya, mai wake anali Hagiti. Mwana wake wachisanu ndi Sefatiya, mai wake anali Abitala. Mwana wake wachisanu ndi chimodzi ndi Itireamu, mai wake anali Egila. Ana asanu ndi mmodzi onseŵa adabadwira ku Hebroni, kumene adakhala mfumu pa zaka zisanu ndi ziŵiri ndi miyezi isanu ndi umodzi. Koma adakhala mfumu ku Yerusalemu zaka 33. Ana amene adabadwira ku Yerusalemu ndi aŵa: Simea, Sobabu, Natani ndi Solomoni. Ameneŵa ndiwo ana anai amene adamubalira Batisuwa mwana wa Amiyele. Panalinso ana aŵa: Ibara, Elisama, Elifeleti, Noga, Nefegi, Yafia, Elisama, Eliyada ndi Elifeleti, ana asanu ndi anai. Onseŵa anali ana a Davide, osaŵerengera ana a azikazi ake. Mlongo wao anali Tamara. Nazi zidzukulu za Solomoni: Rehobowamu adabereka Abiya, Abiya adabereka Asa, Asa adabereka Yehosafati, Yehosafati adabereka Yoramu. Yoramu adabereka Ahaziya, Ahaziya adabereka Yowasi. Yowasi adabereka Amaziya, Amaziya adabereka Azariya, Azariya adabereka Yotamu. Yotamu adabereka Ahazi, Ahazi adabereka Hezekiya, Hezekiya adabereka Manase. Manase adabereka Amoni, Amoni adabereka Yosiya. Ana a Yosiya naŵa: Yohanani, mwana wake wachisamba. Wachiŵiri anali Yehoyakimu, wachitatu anali Zedekiya ndipo wachinai anali Salumu. Ana aamuna a Yehoyakimu anali aŵa: Yekoniya ndi Zedekiya. Ana a Yekoniya, wam'ndende uja, naŵa: Sealatiele, Malikiramu, Pedaya, Senazara, Yekamiya, Hosama, ndiponso Nedabiya. Ana a Pedaya naŵa: Zerubabele ndi Simei. Ana a Zerubabele naŵa: Mesulamu, Hananiya, ndi Selomiti mlongo wao. Panalinso Asuba, Owele, Berekiya, Hasadiya ndi Yusabusede, asanu pamodzi. Ana a Hananiya naŵa: Pelatiya, Yesaya, Refaya, Arinani, Obadiya ndi Sekaniya. Mwana wa Sekaniya anali Semaya. Ana a Semaya naŵa: Hatusi, Igala, Bariya, Neariya ndi Safati, asanu ndi mmodzi. Ana a Neariya, naŵa: Eliyoenai, Hizikiya ndi Azirikamu, atatu. Ana a Eliyoenai, naŵa: Hodaviya, Eliyasibu, Pelaya, Akubu, Yohanani, Delaya ndi Anani, asanu ndi aŵiri. Ana a Yuda naŵa: Perezi, Hezironi, Karimi. Huri ndi Sobala. Reaya mwana wa Sobala adabereka Yahati, Yahati adabereka Ahumai ndi Lahadi. Ameneŵa ndiwo anali mabanja a Azorati. Ana a Huri naŵa: Etamu amene adabereka Yezireele, Isima ndi Idibasi, ndiponso mlongo wao Hazeleleponi; Penuwele amene adabereka Gedori ndi Ezere amene adabereka Husa. Ameneŵa anali ana a Huri, mwana wachisamba wa Efurata ndi tate wa Betelehemu. Asuri amene adabereka Tekowa, anali ndi akazi aŵiri, Hela ndi Nara. Nara adamubalira Ahuzamu, Hefere, Temeni, ndi Haahasitari. Ameneŵa ndiwo anali ana a Nara. Ana a Hela naŵa: Zereti, Izara ndi Etinani. Kozi adabereka Anubu, Zobeba, ndi mabanja a Ahariyele, mwana wa Harumu. Panali munthu wina dzina lake Yabezi amene anthu ankamlemekeza kupambana abale ake. Mai wake pomutcha dzina la Yabezi ankanena kuti, “Chifukwa ndidamubala movutikira.” Yabezi adatama Mulungu wa Israele mopemba kuti, “Mundidalitse ine, ndipo dziko langa mulikuze. Dzanja lanu lamphamvu likhale nane, ndipo mundisunge ine, kuti choipa chisandigwere ndi kumandisautsa.” Motero Mulungu adampatsadi zimene adaapemphazo. Kelubi, mbale wa Suha, adabereka Meiri, Meiri adabereka Esitoni. Esitoni adabereka Beterafa, Paseya ndi Tehina, tate wa Irinahasi. Ameneŵa ndiwo anthu a ku Reka. Ana a Kenazi naŵa: Otiniyele ndi Seraya. Ana a Otiniyele naŵa: Hatati ndi Meonotai. Meonotai adabereka Ofura. Ndipo Seraya adabereka Yowabu, tate wa Ageharasimu. Adaŵatcha choncho popeza kuti anali anthu azaluso. Ana a Kalebe, mwana wa Yefune, naŵa: Iru, Ela, ndi Naamu. Mwana wa Ela anali Kenazi. Ana a Yehalelele naŵa: Zifi, Zifa, Tiriya ndi Asarele. Ana a Ezara naŵa: Yetere, Meredi, Efere ndi Yaloni. Meredi adakwatira Bitiya, mwana wa Farao. Mkaziyo adatenga pathupi nabala Miriyamu, Samai ndi Isiba, bambo wa Esitemowa. Tsono mkazi wake Wachiyuda adamubalira Yeredi, bambo wa Gedori, Hebere bambo wa Soko, ndiponso Yekutiyele bambo wa Zanowa. Ana a mkazi wa Hodiya, mlongo wake wa Nahamu, ndiwo adabereka Keila Mgarimi ndiponso Esitemowa Mmaakati. Ana a Simoni naŵa: Aminoni, Rina, Benihanani ndi Tiloni. Ana a Isi naŵa: Zoheti, ndi Benizoheti. Ana a Sela, mwana wa Yuda, naŵa: Eri, tate wa Leka, Laada, tate wa Maresa ndi wa mabanja a anthu oomba nsalu zabafuta ku Betasebea. Kunalinso Yokimu, pamodzi ndi amuna a ku Kozeba, ndiponso Yowasi ndi Sarafi amene ankalamula ku Mowabu, koma adabwerera ku Lehemu (tsono nkhani zimenezitu nzakalekale). Ameneŵa anali anthu oumba mbiya ndiponso nzika za ku Netaimu ndi ku Gedera. Adakhala kumeneko pamodzi ndi mfumu, namaigwirira ntchito. Ana a Simeoni naŵa: Nemuwele, Yamini, Yaribu, Zera ndi Shaulo. Salumu anali mwana wake, kudzanso Mibisamu ndi Misima. Ana a Misima naŵa: Hamuele kudzanso Zakuli ndi Simei. Simei anali nawo ana aamuna 16, ndi ana aakazi asanu ndi mmodzi. Koma abale ake analibe ana ambiri, ndipo mabanja ao sadakule kufanana ndi anthu a ku Yuda. Iwowo ankakhala ku Beereseba, Molada, Hazara-Suwala, Biliha, Ezemu, Toladi, Betuele, Horoma, Zikilagi, Betemara-Kaboti, Hazara-Susimu, Betebiri ndiponso ku Saaraimu. Imeneyi inali mizinda yao mpaka nthaŵi imene Davide adayamba kulamulira. Ndipo midzi yao inali Etamu, Aini, Rimoni, Tokeni ndi Asani, mizinda isanu, pamodzi ndi midzi yao ina yozungulira mizinda imeneyi, mpaka kukafika ku Baala. Kumeneku ndiko kumene ankakhala ndipo ankasunga mndandanda wa maina. Mesobabu, Yamuleki, Yosa mwana wa Amaziya, Yowele, Yehu mwana wa Yosibiya, mwana wa Seraya, mwana wa Asiyele, Eliyoenai, Yaakoba, Yesohaya, Asaiya, Adiyele, Yesimiele, Benaya, Ziza mwana wa Sifi, mwana wa Aloni, mwana wa Yedaya, mwana wa Simiri ndiponso mwana wa Semaya. Anthu amene tatchulaŵa ndiwo anali atsogoleri a mabanja ao, ndipo mabanja a makolo ao adaonjezeka kwambiri. Motero adapita cha kunja kwa mudzi wa Gedori, kuvuma kwa chigwa, kuti akafunefune busa la ziweto zao. Kumeneko adakapezako busa lokoma ndi la msipu wambiri. Dziko lakenso linali lalikulu, labata ndi laufulu. Anthu amene ankakhala kumeneko kale anali Ahamu. Anthu a fuko a Simeoniwo, ochita kulembedwa maina, adadza pa nthaŵi ya Hezekiya mfumu ya ku Yuda, ndipo adaononga mahema a Ahamuwo ndi kupha Ameuni amene adaŵapeza kumeneko. Adaonongeratu anthu onsewo kotero kuti dzina lao silidamvekenso mpaka lero lino. Kenaka iwowo adakhala ku malo amenewo, popeza kuti kunali msipu womadyetsako ziweto zao. Asimeoni ena okwanira mazana asanu, adapita ku phiri la Seiri. Atsogoleri ao anali Pelatiya, Neyariya, Refaya ndi Uziyele, ana a Isi. Iwowo adaononga Aamaleke otsala amene anali atapulumuka, ndipo adakhala kumeneko mpaka lero lino. Naŵa ana a Rubeni, mwana wachisamba wa Israele. Inde Rubeni analidi mwana wachisamba, koma chifukwa adaagona ndi mkazi wina wamng'ono wa bambo wake, uchisamba wakewo udapatsidwa kwa Yosefe, mng'ono wake. Motero Rubeniyo saoneka pa mndandanda wa maina potsata za kubadwa. Koma a fuko la Yuda anali amphamvu pakati pa mafuko a Israele, ndipo mfumu idachokera kwa iwowo, ngakhale kuti ukulu wa uchisamba unali wa Yosefe. Tsono ana a Rubeni naŵa: Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karimi. Ana a Yowele naŵa: Semaya, Gogi, Simei, Mika, Reaya, Baala, ndi Beera amene Tigilati-Pilesere, mfumu ya ku Asiriya, idamtenga ukapolo. Iyeyo anali mmodzi mwa atsogoleri a Arubeni. Akuluakulu a fuko la Rubeni, potsata mndandanda wa maina ao, naŵa: mtsogoleri Yeiyele, Zekariya, ndiponso Bela mwana wa Azazi, mwana wa Sema, wa banja la Yowele. Onsewo ankakhala ku Aroere mpaka kukafika ku Nebo ndi ku Baala-Meoni. Iwowo adakhala kuvuma mpaka kukafika poloŵera m'chipululu cha mbali ina ya Yufurate, chifukwa chakuti ng'ombe zao zinali zitaswana kwambiri m'dziko la Giliyadi. Pa nthaŵi ya Saulo, Arubeni adathira nkhondo Ahagiri ndi kuŵagonjetsa, kenaka adakhala m'mahema mwao m'dziko lonselo kuvuma kwa Giliyadi. Ana a Gadi adakhala kumpoto kwa Arubeni m'dziko la Basani mpaka kukafika ndithu kuvuma ku Saleka. Mkulu wao anali Yowele, ndipo wachiŵiri wake anali Safani. Panalinso Yanai, ndi Safati ku Basani. Abale ao, potsata mabanja a makolo ao, naŵa: Mikaele, Mesulamu, Sheba, Yorai, Yakani, Ziya ndiponso Eberi, asanu ndi aŵiri. Ameneŵa ndiwo anali ana a Abihaili, mwana wa Huri, mwana wa Yarowa, mwana wa Giliyadi, mwana wa Mikaele, mwana wa Yesisai, mwana wa Yado, mwana wa Buzi. Ahi, mwana wa Abidiyele, mwana wa Guni, ndiye amene anali mfumu ya mabanja a makolo ao. Iwowo adakhala m'midzi ya ku Giliyadi ndi ku Basani ndiponso ku mabusa onse a m'maiko a Saroni mpaka ku mapeto ake. Onseŵa adalembedwa potsata mibadwo yao pa nthaŵi ya Yotamu mfumu ya ku Yuda, ndiponso pa nthaŵi ya Yerobowamu mfumu ya ku Israele. Arubeni, Agadi ndiponso theka la fuko la Manase anali ndi anthu olimba mtima odziŵa kumenya nkhondo ndi zishango, malupanga ndi mauta. Onse pamodzi anali 44,760, okonzekeratu kukamenya nkhondo. Adathira nkhondo Ahagiri, Yeturi, Nafisi, ndiponso Nodabu. Mulungu adaŵathandiza pomenya nkhondoyo, ndipo Ahagiriwo pamodzi ndi onse amene adaaphatikana nawo, adaperekedwa m'manja mwao. Ankalira kwa Mulungu pomenya nkhondoyo, tsono Mulungu adaŵapatsa zimene ankapemphazo, popeza kuti adaamkhulupirira. Adaŵalanda ziŵeto zao monga izi: ngamira zokwanira 50,000, nkhosa zokwanira 250,000, abulu okwanira 2,000. Adagwiranso anthu amoyo okwanira 100,000. Adani ena ambiri adaphedwa, pakuti Mulungu ankaŵathandiza pa nkhondoyo. Choncho anthuwo adakhala bwino kumeneko mpaka nthaŵi yotengedwa ukapolo ija. Theka la fuko la Manase linkakhala m'dziko lakuvuma kuyambira ku Basani mpaka ku Baala-Heremoni, Seniri ndiponso ku phiri la Heremoni. Anthuwo anali ochuluka. Atsogoleri a mabanja a makolo ao anali aŵa: Efere, Isi, Eliyele, Aziriele, Yeremiya, Hodaviya ndiponso Yadiyele. Ameneŵa anali ankhondo amphamvu, anthu omveka, atsogoleri a mabanja a makolo ao. Koma anthu aja adachimwira Mulungu wa makolo ao, nadzipereka kwa milungu ya anthu am'dzikomo amene Mulungu adaŵaononga iwowo akufika. Motero Mulungu wa Israele adautsa mtima wa Pulo mfumu ya ku Asiriya, amene dzina lake lina linali Tigilati-Pilesere, ndipo adaŵatenga Arubeni, Agadi ndiponso theka la fuko la Manase, napita nawo ku Hala, Habori, Hara ndi ku mtsinje wa Gozani, ndipo akukhala kumeneko mpaka lero lino. Ana a Levi naŵa: Geresomo, Kohati, ndi Merari. Ana a Kohati naŵa: Amuramu, Izara, Hebroni ndi Uziyele. Ana a Amuramu naŵa: Aroni, Mose ndi Miriyamu. Ana a Aroni naŵa: Nadabu, Abibu, Eleazara ndi Itamara. Eleazara adabereka Finehasi, Finehasi adabereka Abisuwa, Abisuwa adabereka Buki, Buki adabereka Uzi, Uzi adabereka Zeraya, Zeraya adabereka Meraiyoti, Meraiyoti adabereka Amariya, Amariya adabereka Ahitubi, Ahitubi adabereka Zadoki, Zadoki adabereka Ahimaazi, Ahimaazi adabereka Azariya, Azariya adabereka Yohanani, Yohanani adabereka Azariya (ndi iyeyu uja ankatumikira za unsembe ku nyumba imene Solomoni adamanga ku Yerusalemu). Azariya adabereka Amariya, Amariya adabereka Ahitubi, Ahitubi adabereka Zadoki, Zadoki adabereka Salumu, Salumu adabereka Hilikiya, Hilikiya adabereka Azariya, Azariya adabereka Seraya, Seraya adabereka Yehozadaki. Ndipo Yehozadaki adagwidwa ukapolo nthaŵi imene Chauta adalola Nebukadinezara kuti agwire ukapolo anthu a ku Yuda ndi a mu Yerusalemu. Ana a Levi naŵa: Geresomo, Kohati ndi Merari. Maina a ana a Geresomo naŵa: Libini ndi Simei. Ana a Kohati naŵa: Amuramu, Izara, Hebroni ndi Uziyele. Ana a Merari naŵa: Mali ndi Musi. Mabanja a Levi potsata makolo ao ndi ameneŵa. Ana a Geresomo naŵa: Libini, Yahati ndi Zima, Yowa, Ido, Zera, ndi Yeterai. Ana a Kohati naŵa: Aminadabu, Kora, Asiri, Elikana, Ebiyasafa, Asiri, Tahati, Uriyele, Uziya ndi Shaulo. Ana a Elikana naŵa: Amasai, Ahimoti, Elikana, Zofai, Nabati, Eliyabu, Yerohamu ndi Elikana. Ana a Samuele naŵa: Yowele mwana wake wachisamba, Abiya mwana wake wachiŵiri. Ana a Merari naŵa: Mali, Libini, Simei, Uza, Simea, Hagiya ndi Asaya. Panali anthu ena amene Davide adaŵasankhula kuti azitsogolera mwambo wa nyimbo m'Nyumba ya Chauta, ataikamo Bokosi lachipangano. Ankatumikira akuimba nyimbo pakhomo pa malo opatulika a m'chihema chamsonkhano, mpaka Solomoni atamanga Nyumba ya Chauta ku Yerusalemu. Ndipo ankagwira ntchito yao yotumikirayo potsata malamulo amene adaaŵapatsa. Ameneŵa ndiwo anthu amene ankatumikira pamodzi ndi ana ao aamuna. Pa banja la Kohati panali Hemani, katswiri woimba. Mndandanda wa mibadwo yao unali motere: Hemani anali mwana wa Yowele, mwana wa Samuele. Samuele anali mwana wa Elikana, mwana wa Yerohamu, mwana wa Eliyele, mwana wa Towa. Towa anali mwana wa Zufu, mwana wa Elikana, mwana wa Mahati, mwana wa Amasai. Amasai anali mwana wa Elikana, mwana wa Yowele, mwana wa Azariya, mwana wa Zefaniya. Zefaniya anali mwana wa Tahati, mwana wa Asiri, mwana wa Abiyasafu, mwana wa Kora. Kora anali mwana wa Izara, mwana wa Kohati, mwana wa Levi, mwana wa Israele. Panalinso mbale wake Asafu amene ankatsogolera gulu lachiŵiri la oyimba. Asafuyo anali mwana wa Berekiya, mwana wa Simea. Simea anali mwana wa Mikaele, mwana wa Baaseiya, mwana wa Malikiya. Malikiya anali mwana wa Etini, mwana wa Zera, mwana wa Adaya. Adaya anali mwana wa Etani, mwana wa Zima, mwana wa Simei. Simei anali mwana wa Yahati, mwana wa Geresomo, mwana wa Levi. Etani wa fuko la Merari ankatsogolera gulu lachitatu la oimba. Banja lao likuchokera kwa Levi motere: Etani mwana wa Kisi, mwana wa Abidi, mwana wa Maluki. Maluki anali mwana wa Hasabiya, mwana wa Amaziya, mwana wa Hilikiya. Hilikiya anali mwana wa Amizi, mwana wa Bani, mwana wa Semere. Semere anali mwana wa Mali, mwana wa Musi, mwana wa Merari, mwana wa Levi. Ndipo abale ao Alevi ndiwo amene adasankhidwa kuti azigwira ntchito zonse za m'chihema cha Mulungu. Koma Aroni pamodzi ndi ana ake ankapereka nsembe pa guwa la nsembe zopsereza, ndi pa guwa lofukizirapo lubani. Iwowo ndiwo ankachita ntchito zonse zoyenera malo opatulika kwambiri, ndi kuchita mwambo wolipirira machimo a Aisraele. Ankachita zimenezi potsata zonse zimene Mose mtumiki wa Mulungu adaŵalamula. Ana a Aroni ndi zidzukulu zake naŵa: Eleazara, Finehasi, Abisuwa, Buki, Uzi, Zerahiya, Meraiyoti, Amariya, Ahitubi, Zadoki ndi Ahimaazi. Naŵa malo ao kumene ankakhala potsata malire a malowo: Zidzukulu za Aroni za m'mabanja a Kohati zidalandira chigawo choyamba, ndiye kuti Hebroni, m'dziko la Yuda pamodzi ndi mabusa omwe. Koma minda ndi miraga ya mzindawo adaipatsa Kalebe mwana wa Yefune. Ana a Aroni adaŵapatsa mizinda iyi: Hebroni, mzinda wopulumukiramo uja, ndiponso Libina pamodzi ndi mabusa ake omwe, Yatiri, Esitemowa pamodzi ndi mabusa ake omwe, Hileni pamodzi ndi mabusa ake omwe, Debiri pamodzi ndi mabusa ake omwe, Asani pamodzi ndi mabusa ake omwe, ndiponso Betesemesi pamodzi ndi mabusa ake omwe. Ndipo kuchotsa ku fuko la Benjamini, adaŵapatsa Geba pamodzi ndi mabusa ake omwe, Alemeti pamodzi ndi mabusa ake omwe, ndiponso Anatoti ndi mabusa ake omwe. Mizinda yao yonse, malinga ndi mabanja ao onse, inalipo khumi ndi itatu. Tsono adachita maele ndipo Akohati otsala adaŵagawira midzi khumi kuchokera pa fuko lahafu la Manase. Ageresomo, potsata mabanja ao, adaŵagawira mizinda khumi ndi itatu kuchokera pa mafuko a Isakara, Asere, Nafutali ndiponso Manase ku Basani. Amerari, potsata mabanja ao, adaŵagawira mizinda khumi ndi iŵiri kuchokera pa mafuko a Rubeni, Gadi ndi Zebuloni. Umu ndi m'mene Aisraele adapatsira Alevi mizinda ndi mabusa ake omwe. Atachita maele, adaŵapatsanso mizinda ija imene inali ya mafuko a Yuda, Simeoni ndi Benjamini. Mabanja ena a ana a Kohati adalandira mizinda kuchokera pa fuko la Efuremu. Mizindayo inali iyi: Sekemu, mzinda wopulumukiramo uja, pamodzi ndi mabusa ake ku dziko lamapiri la Efuremu, Gezere pamodzi ndi mabusa ake, Yokomeamu pamodzi ndi mabusa ake, Betehoroni pamodzi ndi mabusa ake, Aiyaloni pamodzi ndi mabusa ake, Gatirimoni pamodzi ndi mabusa ake. Koma mizinda yochokera pa fuko la Manase wakuzambwe, Anere pamodzi ndi mabusa ake, ndiponso Bileamu pamodzi ndi mabusa ake, adaipereka kwa otsala a mabanja a Kohati. Mizinda yochokera pa fuko la Manase wakuvuma, imene Ageresomo adalandira, ndi iyi: Golani ku Basani pamodzi ndi mabusa ake omwe ndiponso Asitaroti pamodzi ndi mabusa ake omwe. Yochokera pa fuko la Isakara ndi iyi: Kedesi pamodzi ndi mabusa ake omwe, Daberati pamodzi ndi mabusa ake omwe, Ramoti pamodzi ndi mabusa ake omwe ndiponso Anemu ndi mabusa ake omwe. Yochokera pa fuko la Asere ndi iyi: Masala pamodzi ndi mabusa ake omwe, Abidoni pamodzi ndi mabusa ake omwe, Hukoki pamodzi ndi mabusa ake omwe, ndiponso Rehobu pamodzi ndi mabusa ake omwe. Yochokera pa fuko la Nafutali ndi iyi: Kedesi wa ku Galilea pamodzi ndi mabusa ake omwe, Hamoni pamodzi ndi mabusa ake omwe, ndiponso Kiriyataimu: pamodzi ndi mabusa ake omwe. Amerari otsala adalandirako mizinda kuchokera pa fuko la Zebuloni: Rimono pamodzi ndi mabusa ake omwe, Tabori pamodzi ndi mabusa ake omwe, Patsidya pa mtsinje wa Yordani ku Yeriko, kuvuma kwa Yordani, mizinda yochokera pa fuko la Rubeni ndi iyi: Bezere kuchigwa pamodzi ndi mabusa ake omwe, Yaza pamodzi ndi mabusa ake omwe, Kedemoti pamodzi ndi mabusa ake omwe ndiponso Mefati pamodzi ndi mabusa ake omwe. Yochokera pa fuko la Gadi ndi iyi: Ramoti ku Giliyadi pamodzi ndi mabusa ake omwe, Mahanaimu pamodzi ndi mabusa ake omwe, Hesiboni pamodzi ndi mabusa ake omwe ndiponso Yazere pamodzi ndi mabusa ake omwe. Ana a Isakara naŵa: Tola, Puwa, Yasubu, ndi Simironi, anai. Ana a Tola naŵa: Uzi, Refaya, Yeriyele, Yamai, Ibisamu, ndi Semuele, atsogoleri a mabanja a makolo ao, ndiye kuti a banja la Tola. Onsewo anali ankhondo amphamvu pa mibadwo yao. Chiŵerengero chao pa nthaŵi ya Davide chinali 22,600. Mwana wa Uzi anali Iziraya. Ana a Iziraya naŵa: Mikaele, Obadiya, Yowele ndiponso Isiya. Asanu onsewo anali atsogoleri. Pamodzi ndi iwowo, malinga ndi mibadwo yao ndi mabanja a makolo ao, panali anthu ankhondo 36,000, pakuti anali ndi akazi ambiri ndiponso ana ambiri. Abale ao a mabanja onse a Isakara analipo onse pamodzi 87,000, ankhondo amphamvu, olembedwa potsata mibadwo yao. Ana a Benjamini naŵa: Bela, Bekere ndiponso Yediyaele, atatu pamodzi. Ana a Bela naŵa: Eziboni, Uzi, Uziyele, Yerimoti ndi Iri, asanu, atsogoleri a mabanja a makolo ao, ankhondo amphamvu. Ndipo chiŵerengero chao potsata mibadwo yao chinali 22,034. Ana a Bekere naŵa: Zimira, Yowasi, Eliyezere, Eliyoenai, Omuri, Yeremoti, Abiya, Anatoti ndi Alemeti. Onseŵa anali ana a Bekere. Ndipo kulembedwa kwao potsata kubadwa kwao ndiponso malinga ndi mibadwo yao, pokhala atsogoleri a mabanja a makolo ao, analipo 20,200, ankhondo amphamvu okhaokha. Mwana wa Yediyaele anali Bilihani. Ana a Bilihani naŵa: Yeusi, Benjamini, Ehudi, Kenana, Zetani, Tarisisi ndi Ahisahara. Onseŵa anali ana a Yediyaele, atsogoleri a mabanja a makolo ao, ankhondo amphamvu 17,200, anthu okonzekera kumenya nkhondo. Supimu ndi Hupimu anali ana a Iri, ndipo analinso a fuko ili. Husimu anali mwana wa Dan. Ana a Nafutali naŵa: Yaziyele, Guni, Yezere ndi Salumu. Anali adzukulu a Biliha. Ana a Manase naŵa: Asiriele amene adamuberekera mzikazi wake wa ku Aramu. Mkazi yemweyo adabalanso Makiri, bambo wake wa Giliyadi. Makiri adapezera Hupimu ndi Supimu akazi, wina wake wina wake. Mlongo wake anali Maaka. Dzina la wachiŵiriyo linali Zelofehadi. Ndipo Zelofehadiyo anali ndi ana aakazi okhaokha. Tsono Maaka, mkazi wa Makiri, adabala mwana wamwamuna, namutcha dzina loti Peresi. Mbale wake anali Seresi, ndipo ana ake aamuna anali Ulamu ndi Rakemu. Mwana wa Ulamu anali Bedani. Ameneŵa anali ana a Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase. Mlongo wake Hamoleketi adabala Isihodi, Abiyezere ndi Mala. Ana a Semida naŵa: Ahiyani, Sekemu, Liki ndi Aniyamu. Zidzukulu za Efuremu nazi: Sutela, Beredi, Tahati, Eleada, Tahati, Zabadi, Sutela. Efuremu anali nawonso ana aŵiri: Ezere ndi Eleadi amene adaphedwa ndi anthu a ku Gati eni ake a dzikolo, chifukwa chakuti adabwera kudzalanda ng'ombe zao. Ndiye Efuremu bambo wao adalira maliro masiku ambiri, choncho abale ake adadza kudzamtonthoza. Pambuyo pake Efuremu adakaloŵa kwa mkazi wake, ndipo mkaziyo adatenga pathupi nabala mwana. Mwanayo adamutcha dzina loti Beriya, chifukwa chakuti tsoka lidaagwera banja lake. Mwana wake wamkazi anali Seera, amene adamanga mzinda wa Betehoroni wakunsi ndi Betehoroni wakumtunda, kudzanso Uzeniseera. Mwana wina wa Efuremu anali Refa, amene zidzukulu zake zinali izi: Resefi, Tela, Tahani, Ladani, Amihudi, Elisama, Nuni ndi Yoswa. Maiko ao kumene ankakhala anali Betele pamodzi ndi midzi yake. Chakuvuma kunali Naarani, chakuzambwe kunali Gezere pamodzi ndi midzi yake, Sekemu pamodzi ndi midzi yake, ndiponso Aya pamodzi ndi midzi yake. Zidzukulu za Manase zinkalamulira mizinda iyi: Beteseani pamodzi ndi midzi yake, Tanaki pamodzi ndi midzi yake, Megido pamodzi ndi midzi yake, Dori pamodzi ndi midzi yake. Kumeneko ndiko kumene kunkakhala ana a Yosefe mwana wa Israele. Ana a Asere naŵa: Imina, Isiva, Isivi, Beriya ndiponso mlongo wao Sera. Ana a Beriya naŵa: Hebere ndi Malakiyele, amene adamanga Birizaiti. Hebere adabereka Yafileti, Somere, Hotamu ndiponso mlongo wao Suwa. Ana a Yafileti naŵa: Pasaki, Bimala ndi Asivati. Ameneŵa ndiwo ana a Yafileti. Ana a Somere mbale wake naŵa: Roga, Yehuba ndiponso Aramu. Ana a Helemu mbale wake naŵa: Zofa, Imina, Selesi ndi Amala. Ana a Zofa naŵa: Suwa, Harenefere, Suwala, Beri, Imira, Bezere, Hodi, Sama, Silisa, Itirani ndi Beera. Ana a Yetere naŵa: Yefune, Pisipa ndi Ara. Ana a Ula naŵa: Ara, Haniyele ndi Riziya. Anthu onseŵa anali zidzukulu za Asere. Anali atsogoleri a mabanja a makolo ao, anthu omveka, ankhondo amphamvu, akuluakulu pakati pa akalonga. Chiŵerengero chao cholembedwa m'buku, potsata mibadwo yao yoyenera ntchito yankhondo, chinali 26,000. Benjamini adabereka Bela mwana wake wachisamba, Asibele mwana wake wachiŵiri, Ahara mwana wake wachitatu, Noha mwana wake wachinai ndi Rafa mwana wake wachisanu. Bela anali ndi zidzukulu izi: Adara, Gera, Abihudi, Abisuwa, Namani, Ahowa, Gera, Sefufani ndiponso Huramu. Ana a Ehudi amene anali atsogoleri a mabanja okhala ku Geba, adachotsedwa kwaoko ndipo adakakhala ku Manahati. Anawo anali Namani, Ahiya ndi Gera. Gerayo amene anali bambo wake wa Uza ndi Ahihudi, ndiye adatsogolera anthu osamutsidwawo. Saharaimu, atachotsa akazi ake Husimu ndi Baara, adakhala ndi ana m'dziko la Mowabu. Mwa mkazi wake Hodesi adabelekamo ana aŵa: Yobabu, Zibiya, Mesa, Malikamu, Yeuzi, Sakiya ndi Mirima. Ameneŵa ndiwo amene anali ana ake, atsogoleri a mabanja. Mwa Husimu adaberekamonso ana aŵa: Abitubu, ndi Elipaala. Ana a Elipaala naŵa: Ebere, Misamu ndi Semedi. Semedi ndiye adamanga mizinda ya Ono ndi Lodi pamodzi ndi midzi yake yomwe. Beriya ndi Sema anali atsogoleri a mabanja okhala ku mzinda wa Aiyaloni. Iwowo adathaŵitsa nzika za ku Gati. Zidzukulu zina za Beriya zinali Ahiyo, Sasaki, Yeremoti, Zebadiya, Aradi, Edere, Mikaele, Isipa ndi Yoha. Zebadiya, Mesulamu, Hiziki, Hebere, Isimerai, Iziliya ndi Yobabu anali zidzukulu za Elipaala. Yakimu, Zikiri, Zabidi, Eliyenai, Ziletai, Eliyele, Adaya, Beraya ndi Simiratu anali zidzukulu za Simei. Isipani, Ebere, Eliyele, Abidoni, Zikiri, Hanani, Hananiya, Elamu, Anitotiya, Ifidea ndi Penuwele, anali zidzukulu za Sasaki. Samuserai, Sehariya, Ataliya, Yaaresiya, Eliya ndi Zikiri anali zidzukulu za Yerohamu. Ameneŵa ndiwo amene anali atsogoleri a mabanja, anthu otchuka potsata mibadwo yao, ndipo onsewo ankakhala ku Yerusalemu. Yeiyele, amene adaamanga Gibiyoni, ankakhala ku Gibiyoni komweko. Mkazi wake anali Maaka. Mwana wake wachisamba anali Abidoni, pambuyo pa iyeyo panali Zuri, Kisi, Baala, Nere, Nadabu, Gedori, Ahiyo, Zekeri, ndi Mikiloti bambo wa Simea). Tsono, monga achibale ao aja, iwoŵanso ankakhala ku Yerusalemu pamodzi ndi achibale aowo. Nere adabereka Kisi, Kisi adabereka Mfumu Saulo, Mfumu Saulo adabereka Yonatani, Malikisuwa, Abinadabu, ndi Esibaala. Yonatani adabereka Meribaala. Meribaala adabereka Mika. Ana a Mika naŵa: Pitoni, Meleki, Tareya ndi Ahazi. Ahazi adabereka Yehoyada, Yehoyada adabereka Alemeti, Azimaveti ndi Zimiri. Zimiri adabereka Moza, Moza adabereka Bineya, Bineya adabereka Rafa, Rafa adabereka Eleasa, Eleasa adabereka Azele. Azele anali ndi ana asanu ndi mmodzi, ndipo maina ao naŵa: Azirikamu, Bokeru, Ismaele, Seyariya, Obadiya ndi Hanani. Onseŵa anali ana a Azele. Ana a mbale wake Eseki naŵa: mwana wake wachisamba Ulamu, wachiŵiri Yeusi, wachitatu Elifeleti. Ana a Ulamu anali ankhondo amphamvu, anthu amauta, ndipo anali ndi ana ndi adzikulu 150. Onseŵa anali Abenjamini. Tsono Aisraele onse adalembedwa potsata mibadwo yao m'buku la mafumu a Aisraele. Anthu a ku Yuda adaatengedwa ukapolo kunka ku Babiloni chifukwa chakuti anali osakhulupirika. Tsono Aisraele oyamba kukakhala m'maiko mwao ndi m'mizinda yao anali anthu wamba, ansembe, Alevi ndi atumiki a ku Nyumba ya Mulungu. Anthu ena a ku Yuda, Benjamini, Efuremu ndi Manase amene ankakhala ku Yerusalemu anali motere: A kwa Ayuda anali aŵa: Utai, mwana wa Amihudi, mwana wa Omuri, mwana wa Imuri, mwana wa Bani, chidzukulu cha Perezi, mwana wa Yuda. A kwa Asiloni anali aŵa: Asaya mwana wachisamba pamodzi ndi ana ake. A kwa Azera anali aŵa: Yeuwele ndi achibale ao, onse pamodzi 690. A kwa Abenjamini anali aŵa: Salu, mwana wa Mesulamu, mwana wa Hodaviya, mwana wa Hasenuwa, Ibineya mwana wa Yerohamu, Ela mwana wa Uzi, mwana wa Mikiri ndiponso Mesulamu, mwana wa Sefatiya, mwana wa Reuwele, mwana wa Ibineya. Ndipo mabanja ao potsata mibadwo yao analipo 956. Onse amene alembedwa pamwambapaŵa anali atsogoleri a mabanja. Mwa ansembe panali Yedaya, Yehoyaribu, Yakini, ndi Azariya mwana wa Hilikiya, mwana wa Mesulamu, mwana wa Zadoki, mwana wa Meraiyoti, mwana wa Ahitubi, mkulu woyang'anira Nyumba ya Mulungu. Panalinso Adaya, mwana wa Yerohamu, mwana wa Pasihuri, mwana wa Malikiya, ndiponso Maasai mwana wa Adiyele, mwana wa Yazera, mwana wa Mesulamu, mwana wa Mesilemiti, mwana wa Imeri. Ansembe amene anali atsogoleri a mabanja analipo 1,760, anthu odziŵa kwambiri ntchito za ku Nyumba ya Chauta. A kwa Alevi naŵa: Semaya mwana wa Hasubu, mwana wa Azirikamu, mwana wa Hasabiya, wa kubanja kwa Merari. Panalinso Bakibakara, Heresi, Galali kudzanso Mataniya, mwana wa Mika, mwana wa Zikiri, mwana wa Asafu. Panalinso Obadiya, mwana wa Semaya, mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni, ndiponso Berekiya, mwana wa Asa, mwana wa Elikana, amene ankakhala ku midzi yoyandikana ndi tauni ya Anetofati. Alonda apamakomo naŵa: Salumu, Akubu, Talimoni, Ahimani pamodzi ndi abale ao (Salumu ndiye anali mtsogoleri,) ndipo mpaka nthaŵi imeneyo, anthu a fukoli adaikidwa kuti azilonda pa khomo lakuvuma la Mfumu. Ameneŵa ndiwo amene kale anali alonda apamakomo ku zithando za Alevi. Salumu mwana wa Kore, mwana wa Ebiyasafu, mwana wa Kora, pamodzi ndi abale ake a ku banja la makolo ake, Akora aja, ankayang'anira ntchito ya utumiki pakhomo pa chihema, monga ankachitira azibambo ao, amene ankayang'anira mudzi wazithando wa Chauta ndi kulonda pa chipata. Finehasi, mwana wa Eleazara ndiye ankaŵalamulira kale. Chauta anali naye! Zekariya mwana wa Meselemiya ankadikira pa khomo la chipata cha chihema chamsonkhano. Onseŵa, amene adasankhidwa kuti akhale alonda apamakomo, analipo 212. Adalembedwa potsata mibadwo yao ku midzi yao. Davide ndi Samuele mneneri ndiwo adaŵaika m'malo ao a ntchito chifukwa cha kukhulupirika kwao. Motero iwowo ndi zidzukulu zao ankayang'anira ndi kumalonda pa makomo a Nyumba ya Chauta, monga ankachitira ku chihema chija. Alondawo anali ku mbali zonse zinai, kuvuma, kuzambwe, kumpoto ndi kumwera. Abale ao amene ankakhala nao m'midzi mwao, ankabwera kamodzikamodzi kudzakhala nao masiku asanu ndi aŵiri, pakuti atsogoleri anai a alonda apamakomo amene anali Alevi, ankayang'anira zipinda ndiponso mosungira chuma cha ku Nyumba ya Chauta. Usiku ankakhala mozungulira Nyumba ya Chauta, pakuti iwowo ndiwo amene adaasenza udindo waulonda, ndipo anali ndi ntchito yotsekula Nyumbayo m'maŵa mulimonse. Ena mwa Aleviwo ankayang'anira ziŵiya za pa chipembedzo, pakuti kunali kofunika kuziŵerenga pozibweza kapena pozitulutsa. Ena mwa iwowo adasankhidwa kuti aziyang'anira zipangizo ndi ziŵiya zina zopatulika. Ena ankayang'anira ufa wosalala, vinyo, mafuta, lubani ndiponso zonunkhira. Koma ndi ansembe amene ankasanganiza zonunkhirazo, ndipo Matitiya, mmodzi mwa Alevi, mwana wachisamba wa Salumu Mkora, ankayang'anira kaphikidwe ka makeke. Abale ao enanso a kwa Akohati ankayang'anira buledi woperekedwa, kuti azimkonza pasabata paliponse. Alevi ena akuluakulu ankayang'anira oimba nyimbo. Iwowo ankakhala m'zipinda m'Nyumba ya Chauta, osamangika ndi ntchito zina, pakuti ankatumikira usana ndi usiku. Onsewo anali atsogoleri a mabanja a makolo a Alevi potsata mibadwo yao, ndipo ankakhala ku Yerusalemu. Yeiyele amene adaamanga mzinda wa Gibiyoni, ankakhala ku Gibiyoni komweko. Mkazi wake anali Maaka. Mwana wake wachisamba anali Abidoni ndipo pambuyo pa iyeyo panali Zuri, Kisi, Baala, Nere, Nadabu, Gedori, Ahiyo, Zekariya ndi Mikiloti, bambo wa Simea. Tsono, monga achibale ao aja, iwoŵanso ankakhala ku Yerusalemu pamodzi ndi achibale aowo. Nere adabereka Kisi, Kisi adabereka Saulo, Saulo adabereka Yonatani, Malikisuwa, Abinadabu, ndi Esibaala. Yonatani anabereka Meribaala. Meribaala adabereka Mika. Ana a Mika naŵa: Pitoni, Meleki, Tareya ndi Ahazi. Ahazi adabereka Yara, Yara adabereka Alemeti, Azimaveti ndi Zimiri. Zimiri adabereka Moza. Moza adabereka Bineya, Bineya adabereka Rafaya, Rafaya adabereka Eleasa, Eleasa adabereka Azele. Azele anali ndi ana asanu ndi mmodzi ndipo maina ao naŵa: Azirikamu, Bokeru, Ismaele, Seyariya, Obadiya ndi Hanani. Onseŵa anali ana a Azele. Afilisti adamenyananso nkhondo ndi Aisraele, ndipo Aisraele adathaŵa Afilisti; ambiri adakaphedwa ku phiri la Gilibowa. Afilistiwo adapanikiza Saulo ndi ana ake, ndipo adapha Yonatani, Abinadabu ndi Malikisuwa ana a Saulo. Nkhondo idampanikiza kwambiri Sauloyo, ndipo anthu amauta adampeza namlasa koopsa. Pamenepo Saulo adauza wonyamula zida zake kuti, “Solola lupanga lako, undibaye, kuwopa kuti anthu osaumbalidwaŵa akabwera angadzandiseke.” Koma wonyamula zida uja sadathe kuchita zimenezo, chifukwa ankachita mantha kwambiri. Ndiye Saulo adangotenga lupanga lake nagwerapo. Wonyamula zida uja ataona kuti Sauloyo wafa, nayenso adadzigwetsa pa lupanga lake, nkufa. Umu ndimo m'mene adafera Saulo, iyeyo ndi ana ake atatu, pamodzi ndi banja lake lonse. Aisraele onse amene anali ku chigwa, ataona kuti gulu lankhondo lathaŵa, ndipo kuti Saulo ndi ana ake aphedwa, nawonso adathaŵa nasiya mizinda yao. Tsono Afilisti aja adabwera nkudzakhala m'menemo. M'maŵa mwake, Afilisti atabwera kudzafunkha za anthu ophedwawo, adapeza Saulo ataphedwa pamodzi ndi ana ake pa phiri la Gilibowa. Adamdula mutu Sauloyo, namuvula zida zake zankhondo. Kenaka adatuma amithenga ku dziko lao lonse, kuti akafalitse uthenga wabwinowu kwa milungu yao ndi kwa anthu omwe. Tsono adaika zida za Sauloyo m'nyumba ya milungu yao, ndipo adakhomerera mutu wakewo ku nyumba ya Dagoni, mulungu wao. Koma anthu a ku Yabesi-Giliyadi atamva zonse zimene Afilisti adaamchita Saulo, amuna onse olimba mtima adanyamuka kukatenga mtembo wa Saulo ndi mitembo ya ana ake kubwera nayo ku Yabesi. Adakwirira mafupa aowo patsinde pa mtengo wa thundu ku Yabesi, ndipo adasala zakudya masiku asanu ndi aŵiri. Choncho Saulo adafa chifukwa cha kusakhulupirika kwake. Iyeyo anali wosakhulupirika kwa Chauta, poti sankamvera mau a Chauta ndiponso ankapempha nzeru kwa anthu olankhula ndi mizimu, ndipo sankafuna kuti Chauta amutsogolere. Nchifukwa chake Chautayo adamupha napereka ufumu kwa Davide mwana wa Yese. Aisraele onse adadzasonkhana kwa Davide ku Hebroni. Adamuuza kuti, “Ifetu ndi inuyo tili magazi amodzi. Kale, ngakhale Saulo adakali mfumu yathu yotilamulira, ndinuyo amene munkatsogolera Aisraele ku nkhondo, nkumabwera nawonso. Ndipo Chauta, Mulungu wanu, adaakuuzani kuti, ‘Udzakhala mbusa wa anthu anga Aisraele, udzakhala mfumu ya anthu anga Aisraele.’ ” Choncho atsogoleri onse a Aisraele adadza kwa mfumu ku Hebroni. Tsono Davide adachita nawo chipangano pamaso pa Chauta ku Hebroniko, ndipo anthuwo adamdzoza Davideyo kuti akhale mfumu ya Aisraele onse, potsata mau a Chauta ochokera m'kamwa mwa Samuele. Pambuyo pake Davide pamodzi ndi Aisraele onse adapita kukathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu, ndiye kuti Yebusi, kumene kunkakhala Ayebusi nzika za dzikolo. Ayebusiwo adauza Davide kuti, “Kuno sudzaloŵako ai.” Komabe Davideyo adalanda linga la Ziyoni, ndiye kuti Mzinda wa Davide. Davide anali atanena kuti, “Aliyense amene ayambe kukantha Ayebusi, adzakhala mkulu wolamulira gulu lankhondo.” Tsono Yowabu mwana wa Zeruya ndiye adayamba kupitako, motero adakhala mtsogoleri wankhondo woyamba. Popeza kuti Davide ankakhala m'lingamo, lingalo linkatchedwa Mzinda wa Davide. Ndipo adamanga mzinda kuzungulira deralo kuyambira ku linga la Milo mpaka m'kati mwake. Yowabu ndiye adakonza mbali ina ya mzindawo. Motero mphamvu za Davide zidanka zikulirakulira, chifukwa Chauta wamphamvuzonse anali naye. Tsono aŵa ndiwo atsogoleri a nkhondo a Davide, amene ankamthandiza pamodzi ndi Aisraele onse, kuti akhale mfumu potsata mau a Chauta onena za Israele. Mndandanda wa anthu amphamvu a Davide ndi uwu: Yasobeamu Muhakimoni ndiye amene anali wamkulu mwa atsogoleri a anthu aja. Tsiku lina adapha ndi mkondo wake anthu 300 nthaŵi imodzi. Mnzake wotsatana naye mwa anthu atatu amphamvu aja anali Eleazara, mwana wa Dodo, Mwahohi. Iyeyo anali pamodzi ndi Davide ku Pasidamimu pamene Afilisti adaasonkhana kumeneko kuti amenyane naye nkhondo. Kumeneko kudaali munda wodzaza ndi barele ndipo anthu a Davide adathaŵa kuwopa Afilistiwo. Koma Eleazara ndi anzake adakaima m'kati mwa mundawo nautchinjiriza, ndipo adapha Afilistiwo. Motero Chauta adaŵapulumutsa ndi kuŵapambanitsa kwambiri. Tsiku lina atatu mwa atsogoleri makumi atatu aja adatsikira ku thanthwe mpaka kwa Davide ku phanga la Adulamu. Kufupi nkumeneko ankhondo a Afilisti anali atamanga zithando zankhondo ku chigwa cha Refaimu. Pamenepo nkuti Davide ali m'phanga muja, ndipo kagulu kankhondo ka Afilisti kanali ku Betelehemu. Ndiye Davide atamva ludzu kwambiri adati, “Ha, wina akadandipatsa madzi a m'chitsime chimene chili pafupi ndi chipata ku Betelehemu kuti ndimwe!” Pomwepo anthu atatu amphamvu aja adapita akubzola zithando za Afilisti, nakatunga madzi ku chitsime cha ku Betelehemu, chimene chinali pafupi ndi chipata. Adatenga madziwo nabwera nawo kwa Davide. Koma Davideyo sadafune kumwako madziwo, adangoŵathira pansi kuŵapereka kwa Chauta. Ndipo adati, “Ndithu, pali Mulungu, sindingachite chinthu chotere, chifukwa kukhala ngati kumwa magazi a anthuŵa amene adaika moyo wao pa minga, pang'ono akadataya moyo wao pokabwera nawo madzi ameneŵa.” Motero adakana kumwa madziwo. Zimenezi ndizo adachita anthu atatu amphamvu aja. Abisai, mbale wake wa Yowabu, anali mkulu wa atsogoleri makumi atatu aja. Ndiye adapha ndi mkondo wake anthu 300, nakhala wotchuka ngati anthu atatu aja. Iye anali womveka kwambiri mwa atsogoleri makumi atatu aja, ndipo adasanduka mkulu wao, komabe sadafikepo pa anthu atatu aja. Benaya mwana wa Yehoyada wa ku Kabizeele, anali munthu wolimba mtima, amene ankachita ntchito zazikulu. Iyeyo adapha ngwazi ziŵiri za ku Mowabu. Tsiku lina chisanu cha mbee chitagwa adatsikira m'chitsime, naphamo mkango. Adaphanso Mwejipito wina wamkulu thupi, kutalika kwake ngati mamita aŵiri ndi theka. Mwejipitoyo anali ndi mkondo m'manja wofanafana ndi mtanda wa munthu woomba nsalu. Koma Benaya adapita kwa iyeyo atatenga ndodo, nalanda mkondowo kumanja kwa Mwejipito uja, nkumupha ndi mkondo wake womwewo. Zimenezi ndizo adachita Benaya mwana wa Yehoyada, ndipo adatchuka ngati atsogoleri makumi atatu amphamvu aja. Iyeyu anali womveka mwa atsogoleri makumi atatuwo, komabe sadafikepo pa anthu atatu aja. Davide adamuika kuti azilamulira asilikali ake omuteteza. Anthu amphamvu a m'magulu ankhondowo anali aŵa: Asahele mbale wa Yowabu, Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu, Samoti wa ku Harodi, Helezi Mpeloni, Ira mwana wa Ikesi wa ku Tekowa, Abiyezere wa ku Anatoti, Sibekai Muhusati, Ilai Mwahohi, Maharai wa ku Netofa, Heledi mwana wa Baana wa ku Netofa, Itai mwana wa Ribai wa ku Gibea, Mbenjamini. Panalinso Benaya wa ku Piratoni, Hurai wa ku mitsinje ya ku Gaasi, Abiyele Mwarabati, Azimaveti wa ku Baharumi, Eliyaba wa ku Saaliboni, Hasemu Mgizoni, Yonatani mwana wa Sage Muharari, Ahiyamu mwana wa Sakara Muharari, Elifala mwana wa Uri, Hefere Mmekerati, Ahiya Mpeloni, Heziro wa ku Karimele, Naarai mwana wa Ezibai, Yowele mbale wake wa Natani, Mibara mwana wa Hagiri, Zeloki Mwamoni, Naharai wa ku Beeroti, wonyamula zida za Yowabu mwana wa Zeruya, Ira Mwitiri, Garebu Mwitiri, Uriya Muhiti, Zabadi mwana wa Alai, Adina mwana wa Siza Mrubeni, mtsogoleri wa Arubeni, ndi anthu makumi atatu pamodzi naye, Hanani mwana wa Maaka, ndiponso Yosafati Mmitini, Uziya Mwasiterati, Sama ndi Yeiyele ana a Hotamu Mweroeri, Yediyaele mwana wa Simiri, ndi Yoha mbale wake Mtizi, Eliyele Mmahavi, ndiponso Yeribai ndi Yosaviya, ana a Elinamu, kudzanso Itima Mmowabu, Eliyele, Obede ndi Yaasiyele Mmezobai. Naŵa anthu amene adadza kwa Davide ku Zikilagi, kumene Davideyo adaathaŵira chifukwa choopa Saulo mwana wa Kisi. Anthu ameneŵa ankathandiza Davide kumenya nkhondo, pamodzi ndi anzao amphamvu. Iwoŵa anali anthu odziŵa kugwiritsa ntchito uta. Mivi ndi miyala ankatha kuponyera dzanja lamanja kapena lamanzere. Iwoŵa anali Abenjamini, abale ake a Saulo. Mtsogoleri wao anali Ahiyezere, wotsatana naye anali Yowasi. Aŵiri onsewo anali ana a Semaa wa ku Gibea. Panalinso Yeziyele ndi Peleti, ana a Azimaveti, Beraka, Yahu wa ku Anatoti, ndi Isimaya wa ku Gibiyoni, amene anali wamphamvu mwa anthu makumi atatu aja ndiponso mmodzi mwa atsogoleri ao. Panalinso Yeremiya, Yahaziele, Yohanani, Yozabadi wa ku Gedera, Eluzai, Yeremoti, Bealiya, Semariya, Sefatiya wa ku Harufi, Elikana, Isiya, Azarele, Yowezere, ndiponso Yasobeamu. Onsewo anali Akora. Panalinso Yowela ndi Zebadiya, ana a Yerohamu wa ku Gedori. Asilikali ena amphamvu, ochokera ku dziko la Gadi, adafika kwa Davide ku linga lake lam'chipululu. Iwoŵa anali ngwazi zodziŵa kumenya nkhondo, makamaka pogwiritsa ntchito chishango ndi mkondo, ndipo anali oopsa ngati mikango. Akamathamanga, ngati ngoma zam'mapiri liŵiro lake. Ezere anali mtsogoleri, wachiŵiri anali Obadiya, wachitatu Eliyabu, wachinai Misimana, wachisanu Yeremiya, wachisanu ndi chimodzi Atai, wachisanu ndi chiŵiri Eliyele, wachisanu ndi chitatu Yohanani, wachisanu ndi chinai Elizabadi, wa 10 Yeremiya, wa 11 Makibanai. Agadi ameneŵa ndiwo amene anali m'gulu la atsogoleri ankhondo. Ang'onoang'ono ankalamulira anthu 100, pamene akuluakulu ankalamulira anthu 1,000. Ameneŵa ndiwo anthu amene adaoloka Yordani mwezi woyamba, nthaŵi imene mtsinjewo unali wodzaza nkumasefukira pa zibumi zake zonse. Motero adapirikitsa anthu onse amene anali m'zigwa. Ena kuthaŵira kuvuma ena kuzambwe. Tsiku lina anthu ena a ku Benjamini ndi a ku Yuda adadza ku linga la Davide. Davide adatuluka kukakumana nawo, ndipo adaŵauza kuti, “Ngati mwadza kwa ine kuno mwaubwenzi kuti mudzandithandize, ndiye kuti mtima wanga udzagwirizana nanu. Koma ngati nkundipereka kwa adani anga, ngakhale sindidalakwe, pamenepo Mulungu wa makolo athu apenye ndipo akulangeni.” Pomwepo Mzimu wa Mulungu udamtsikira Amasai, mtsogoleri wa anthu makumi atatu aja, ndipo adati, “Inu Davide, ifetu ndife anu. Tili limodzi nanu, inu mwana wa Yese. Inu ndi anthu amene amakuthandizani, mudzakhala opambana. Zoonadi Mulungu wanu ali nanu.” Tsono Davide adaŵalandira ndipo adaŵasandutsa atsogoleri a magulu ake ankhondo. Anthu ena a fuko la Manase adabwera kwa Davide nthaŵi imene Davide adadza ndi Afilisti kudzamenyana nkhondo ndi Saulo. Komabe nthaŵiyo Davide sadaŵathandize Afilisti, poti akazembe ao adambweza namanena kuti, “Uyu akhoza kubwerera kwa mbuye wake Saulo, ndiye ife tidzaonongeka pamenepo.” Motero pamene Davide ankabwerera ku Zikilagi, anthu a fuko la Manase aja adapita naye limodzi. Amanasewo anali aŵa: Adina, Yozabadi, Yediyaele, Mikaele, Yozabadi, Elihu ndi Ziletai, atsogoleri a magulu a ankhondo zikwi zambiri a ku Manase. Iwoŵa adathandiza Davide kulimbana ndi magulu a achifwamba, pakuti onseŵa anali anthu amphamvu, olimba mtima, ndipo anali atsogoleri pa nkhondo. Anthu ankabwera kwa Davide tsiku ndi tsiku kudzamthandiza, mpaka gulu lake lankhondo lidakula kwambiri, ngati gulu lankhondo la Mulungu. Nachi chiwerengero cha magulu a anthu ankhondo amene adadza ku Hebroni kwa Davide, kudzamlonga ufumu m'malo mwa Saulo, potsata mau a Chauta. Ankhondo a ku Yuda ogwira zishango ndi mikondo analipo 6,800. A fuko la Simeoni, anthu amphamvu olimba mtima pomenya nkhondo, 7,100. A fuko la Levi, 4,600. Mtsogoleri Yehoyada wa banja la Aroni adabwera ndi anthu 3,700. Zadoki mnyamata wolimba mtima adabwera ndi achibale ake 22. A fuko la Benjamini, abale ake a Saulo, analipo 3,000. Koma mpaka pa nthaŵi imeneyo, ambiri mwa iwowo ankaumirirabe kumatsata banja la Saulo. A banja la Efuremu, 20,800 anthu amphamvu ndi olimba mtima, anthu omveka ku mabanja a makolo ao. A fuko lahafu la Manase analipo 18,000, amene adaachita kuŵaitana kuti adzalonge nao ufumu Davide. A fuko la Isakara analipo atsogoleri 200 pamodzi ndi anthu ao. Atsogoleriwo ankamvetsa zinthu pa nthaŵi imeneyo, namadziŵa zimene Israele ankayenera kuchita pa nthaŵi yake. A fuko la Zebuloni analipo 50,000 asilikali okonzekera nkhondo, okhala ndi zida zankhondo zamitundumitundu, othandiza Davide ndi mtima umodzi. A fuko la Nafutali, atsogoleri 1,000 amene anali ndi asilikali 37,000 a zishango ndi mikondo. A fuko la Dani, anthu 28,600 okonzekera kumenya nkhondo. A fuko la Asere anali 40,000, ankhondo enieni, okonzekera kumenya nkhondo. A fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi fuko lahafu la Manase, kuchokera pa tsidya ilo la mtsinje wa Yordani, analipo 120,000 odziŵa kumenya nkhondo ndi zida zosiyanasiyana. Ankhondo onseŵa amene ankadziŵa kamenyedwe ka nkhondo, adadza ku Hebroni ndi mtima umodzi, kuti akamlonge ufumu Davide. Aisraele onse nawonso anali ndi mtima womwewo wofuna kumlonga ufumu Davide. Ndipo adakhala komweko masiku atatu pamodzi ndi Davide namadya zimene abale ao anali ataŵakonzekera. Nawonso anansi ao, ochokera ngakhale ku Isakara ndi Zebuloni ndi Nafutali, adadza atasenzetsa chakudya abulu ao, ngamira zao, nyulu zao ndi ng'ombe zao. Adazisenzetsa chakudya chambiri, makeke ankhuyu, ntchichi zamphesa, vinyo ndiponso mafuta. Adabweranso ndi ng'ombe ndi nkhosa zambiri, poti ku dziko la Israele kunali chisangalalo. Davide adapempha nzeru kwa atsogoleri a anthu zikwi, kwa atsogoleri a anthu mazana, ndi kwa mtsogoleri wina aliyense. Pambuyo pake adauza msonkhano wonse wa Aisraele kuti, “Ngati zikukukomerani inu, ndipo ngati chimenecho ndiye chifuniro cha Chauta, Mulungu wathu, tiyeni titumize mau kwa abale athu onse amene akukhala m'dziko lonse la Israele ndiponso kwa ansembe ndi kwa Alevi okhala ku mizinda ndi ku miraga yake, kuti anthuwo adzasonkhane pamodzi kwa ife kuno. Tsono tibwere nalonso bokosi lachipangano la Chauta wathu. Paja pa nthaŵi ya Saulo sitidalisamale Bokosilo.” Msonkhano wonse udavomereza zimenezo, poti anthu onse adaaona kuti nzabwino. Choncho Davide adasonkhanitsa Aisraele onse kuyambira ku mtsinje wa Sihori ku Ejipito mpaka ku chipata cha Hamati, kuti abwere nalo Bokosi lachipangano la Mulungu kuchokera ku Kiriyati-Yearimu. Ndipo Davide pamodzi ndi Aisraele onse adakwera kupita ku Baala, ndiye kuti ku Kiriyati-Yearimu m'dera la ku Yuda, kuti akatenge Bokosi lachipangano la Mulungu. Bokosilo limadziŵika ndi dzina la Chauta amene amakhala pa akerubi ngati pa mpando waufumu. Bokosi lachipanganolo adalinyamula pa ngolo yatsopano, kuchoka nalo ku nyumba ya Abinadabu. Uza ndi Ahiyo ndiwo amene ankayendetsa ngoloyo. Tsono Davide pamodzi ndi Aisraele onse anali ankakondwera kwambiri kulemekeza Mulungu poimba nyimbo ndi azeze, apangwe ndi ting'oma, ziwaya zamalipenga ndi malipenga amene. Tsono atafika ku malo ophunthirapo tirigu ku Kidoni, ng'ombe zidaafuna kugwetsa Bokosi lija, ndiye Uza nkutambalitsa dzanja kuti aligwirire Bokosilo. Pomwepo Chauta adampsera mtima Uzayo namkantha chifukwa chakuti adatambalitsa dzanja lake nakhudza Bokosi lija. Adafera pomwepo pamaso pa Chauta. Tsono Davide adakhumudwa chifukwa chakuti Chauta adaakantha Uza. Ndipo mpaka pano malo amenewo amaŵatchula kuti Pereziuza. Davide adachita mantha ndi Mulungu tsiku limenelo, ndipo adafunsa kuti, “Kodi ndingathe bwanji kufika nalo kwathu Bokosi la Mulunguli?” Motero sadabwere nalo Bokosilo kwao ku mzinda wa Davide, koma adalipatutsira ku nyumba ya Obededomu Mgiti. Choncho Bokosi lachipanganolo lidakhala miyezi itatu kwa Obededomu, m'nyumba mwake. Ndipo Chauta adadalitsa banja la Obededomu pamodzi ndi zonse zimene adaali nazo. Hiramu, mfumu ya ku Tiro, adatuma amithenga kwa Davide, pamodzi ndi mitengo ya mkungudza ndiponso amisiri odziŵa kumanga ndi miyala ndi amisiri a matabwa, kuti akammangire nyumba Davideyo. Motero Davide adazindikira kuti Chauta wamkhazikitsa kuti akhale mfumu yolamulira Aisraele, ndiponso kuti wakweza ufumu wake chifukwa cha Aisraele, anthu ake. Davide adakwatira akazi ena ku Yerusalemu, ndipo adabereka ana enanso aamuna ndi aakazi. Ana amene Davide adaberekera ku Yerusalemu ndi aŵa: Samuwa, Sobabu, Natani, Solomoni, Ibara, Elisuwa, Elipeleti, Noga, Nefegi, Yafiya, Elisama, Beeliyada, ndi Elifeleti. Afilisti atamva kuti Davide wadzozedwa kukhala mfumu yolamulira dziko lonse la Aisraele, adapita onse kukamfunafuna. Davide atamva zimenezo, adatuluka kukamenyana nawo nkhondo. Tsono Afilisti adafika nayamba kufunkha m'chigwa cha Refaimu. Pamenepo Davide adafunsa kwa Mulungu kuti, “Kodi ndipite kukamenyana nawo nkhondo Afilistiwo? Kodi mudzaŵapereka m'manja mwanga?” Chauta adamuuza kuti, “Inde, pita. Ndidzaŵaperekadi m'manja mwako.” Pamenepo Davide adapita ku Baala-Perazimu, ndipo adagonjetsa Afilistiwo kumeneko. Tsono adati, “Ndi dzanja langa Mulungu waŵang'amba pakati adani anga ngati madzi a chigumula.” Nchifukwa chake malo amenewo amatchedwa kuti Baala-Perazimu. Afilistiwo adasiya milungu yao kumeneko ndipo Davide adalamula kuti aiyatse moto, ndipo adaitenthadi. Nthaŵi ina Afilistiwo adabweranso naloŵa m'chigwa mom'muja. Davide atafunsanso Mulungu, Mulungu adamuuza kuti, “Usati uŵalondole. Uchite moŵazungulira, uŵadzere cha kumbuyo, uŵathire nkhondo pa malo oyang'anana ndi mitengo ya mkandankhuku ija. Tsono ukakamva phokoso pa nsonga za mitengo ya mkandankhukuyo, pamenepo utuluke kukamenyana nawo. Pakuti Mulungu wakutsogolera kuti ukakanthe gulu lankhondo la Afilistiwo.” Davide adachitadi monga momwe Mulungu adaamlamulira, ndipo adagonjetsa gulu lankhondo la Afilistilo kuyambira ku Gibiyoni mpaka ku Gezere. Ndipo mbiri ya Davide idawanda ku maiko onse, ndipo Ambuye adachititsa mantha anthu a mitundu yonse kuti azimuwopa Davideyo. Davide adadzimangira nyumba zina mu mzinda wa Davide. Adakonza malo a Bokosi lachipangano la Chauta, namanga hema loikamo Bokosilo. Tsono Davide adati, “Alevi okha ndiwo amene asenze Bokosi lachipangano la Mulungu, wina aliyense ai, pakuti Chauta adasankhula Aleviwo kuti azisenza Bokosilo ndiponso kuti azimtumikira mpaka muyaya.” Kenaka Davide adasonkhanitsa Aisraele onse ku Yerusalemu, kuti akatenge Bokosi lachipangano la Chauta ndi kubwera nalo ku malo ake amene Davideyo adalikonzera. Tsono Davide adasonkhanitsa zidzukulu za Aroni ndi Alevi enanso. Mwa ana a Kohati, Uriyele ndiye anali mtsogoleri, ndipo iye ndi abale ake, onse analipo 120. Mwa ana a Merari, Asaya ndiye anali mtsogoleri, ndipo iye ndi abale ake, onse analipo 220. Mwa ana a Geresomo, Yowele ndiye anali mtsogoleri, ndipo iye ndi abale ake, onse analipo 130. Mwa ana a Elizafani, Semaya ndiye anali mtsogoleri, ndipo iye ndi abale ake, onse analipo 200. Mwa ana a Hebroni, Eliyele ndiye anali mtsogoleri, ndipo iye ndi abale ake, onse analipo 80. Mwa ana a Uziyele, Aminadabu ndiye anali mtsogoleri, ndipo iye ndi abale ake, onse analipo 112. Tsono Davide adaitana ansembe aŵa Zadoki ndi Abiyatara, kudzanso Alevi aŵa, Uriyele, Asaya, Yowele, Semaya, Eliyele ndi Aminadabu. Ndipo adaŵauza kuti, “Inuyo ndinu atsogoleri a mabanja a makolo a Alevi. Mudzipatule eniakenu ndi abale anu omwe, kuti musenze Bokosi lachipangano la Chauta, Mulungu wa Aisraele, ndipo mukaliike ku malo amene ndidalikonzera. Popeza kuti simudalinyamule ndinu poyamba paja, Chauta adatikantha, chifukwa choti sitidasamale mwambo wake polinyamula.” Motero ansembe ndi Alevi aja adadzipatula kuti akanyamule Bokosi lachipangano la Chauta, Mulungu wa Aisraele. Ndipo Alevi adanyamula ndi mphiko Bokosilo pamapuzi pao, monga momwe Mose adaalamulira potsata mau a Chauta. Pambuyo pake Davide adalamulanso atsogoleri a Alevi kuti asankhe ena mwa abale ao, kuti aziimba ndi kuliza mwamphamvu zipangizo zoimbira monga azeze, apangwe, ndiponso ziwaya zamalipenga, kuti mau achimwemwe amveke bwino. Motero Alevi adasankha Hemani mwana wa Yowele, ndipo mwa abale ake adasankha Asafu mwana wa Berekiya. Mwa ana a Merari, abale ao, adasankha Etani mwana wa Kusaya. Pamodzi ndi iwowo, otsatana nawo osankhidwanso anali Zekariya, Yaaziyele, Semiramoti, Yehiyele, Uni, Eliyabu, Benaya, Maaseiya, Matitiya, Elifelehu ndiponso Mikineya, kudzanso alonda apamakomo, Obededomu ndi Yeiyele. Anthu oimba aja, Hemani, Asafu ndi Etani ndiwo amene ankaimba ziwaya zamalipenga zamkuŵa. Zekariya, Aziyele, Semarimoti, Yehiyele, Uni, Eliyabu, Maaseiya ndi Benaya ndiwo amene ankaimba azeze a liwu lapamwamba. Koma Matitiya, Elibelehu, Mikineya, Obededomu, Yeiyele ndiponso Azaziya ndiwo amene ankatsogolera, namaimba apangwe a liwu lapansi. Kenaniya, mtsogoleri wa Alevi poimba nyimbo, ndiye amene ankatsogolera kuimbako, poti anali katswiri. Benekiya ndi Elikana ndiwo adasankhidwa kuti akhale alonda apakhomo olonda Bokosilo. Ansembe aŵa, Sebaniya, Yosafati, Netanele, Amasai, Zekariya, Benaya ndi Eliyezere ndiwo ankayenera kuliza malipenga patsogolo pa Bokosi lachipangano la Mulungu. Obededomu ndi Yehiya nawonso anali alonda apakhomo a Bokosilo. Motero Davide pamodzi ndi akuluakulu a Aisraele ndiponso atsogoleri a ankhondo zikwi-zikwi, adapita mokondwera kuti akatenge Bokosi lachipangano la Chauta kunyumba kwa Obededomu. Pofuna kuti Mulungu aŵathandize Alevi amene ankanyamula Bokosilo, anthuwo adaperekera nsembe ng'ombe zamphongo zisanu ndi ziŵiri ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziŵiri. Davide anali atavala mkanjo wabafuta wa thonje losalala, monga momwe adavalira Alevi amene ankanyamula Bokosi lachipangano, kudzanso anthu oimba ndiponso Kenaniya mtsogoleri wa anthu oimba nyimbo. Koma Davide adaavalanso efodi. Motero Aisraele onse adabwera nalo Bokosi lachipangano la Chauta akufuula ndi kuimba mbetete, malipenga ndi ziwaya zamalipenga. Ankalizanso azeze ndi apangwe mokweza. Pamene Bokosi lachipangano lija lidadza ku mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Saulo, adasuzumira pa windo, naona mfumu Davide akulumphalumpha ndi kuvina. Pamenepo mkaziyo adayamba kunyoza Davide mumtima mwake. Anthu adaloŵa nalo Bokosi lachipangano lija, nalikhazika pamalo pake m'kati mwa hema limene Davide adaamangira Bokosilo. Tsono adapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano kwa Mulungu. Davide atamaliza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjanozo, adadalitsa anthu onse m'dzina la Chauta. Kenaka adagaŵira Aisraele onsewo, amuna ndi akazi, aliyense mtanda wa buledi, nthuli ya nyama ndiponso keke ya mphesa zouma. Ndipo adaika Alevi ena kuti azitumikira ku Bokosi lachipangano la Chauta, ndiye kuti azipemphera, azithokoza ndi kumatamanda Chauta, Mulungu wa Israele. Asafu ndiye amene anali mtsogoleri, ndipo omthandiza wake anali Zekariya, Yeiyele, Semiramoti, Yehiyele, Matitiya, Eliyabu, Benaya, Obededomu ndi Yeiyele. Ameneŵa ndiwo adasankhindwa kuti akhale oliza azeze ndi apangwe. Asafu ndiye amene anali woliza ziwaya zamalipenga, ndipo Benaya ndi Yehaziele, ansembe, ndiwo amene anali oliza malipenga nthaŵi zonse patsogolo pa Bokosi lachipangano la Chauta. Tsiku limenelo ndi limene Davide adayamba kulamula Asafu ndi abale ake kuti akhale oyang'anira nyimbo zothokoza Chauta. Thokozani Chauta, tamandani dzina lake, lalikani za ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu. Imbirani Chauta, muimbireni nyimbo zomtamanda, lalikani za ntchito zake zodabwitsa. Munyadire dzina lake loyera. Ikondwe mitima ya anthu amene amapembedza Chauta. Muzidalira Chauta ndi mphamvu zake. Muziyesetsa kukhala pamaso pake kosalekeza. Muzikumbukira ntchito zodabwitsa za Chauta, zozizwitsa zimene adachita, ndi m'mene ankaweruzira anthu, inu zidzukulu za Abrahamu mtumiki wake, inu ana a Yakobe, osankhidwa a Chauta. Iye ndiye Chauta, Mulungu wathu. Amalamulira dziko lonse lapansi. Muzikumbukira chipangano chake nthaŵi zonse, musaiŵale mpaka muyaya mau amene Iye adalamula, Amakumbikira chipangano adachita ndi Abrahamu chija, lonjezo lake limene adachita molumbira kwa Isaki. Lonjezolo adabwerezanso kwa Yakobe, kuti likhale chipangano chokhazikika mu Israele mpaka muyaya. Adati, “Ndidzakupatsa dziko la Kanani, kuti likhale choloŵa chako chokhalira iweyo.” Pamene anali anthu oŵerengeka, anthu osatchuka, ongokhala nao m'dzikomo, ongomayendayenda kuchokera ku mtundu wina wa anthu kupita ku mtundu wina, kuchokera ku ufumu wina kupita ku ufumu wina, sadalole ndi mmodzi yemwe aŵapsinje, adalanga mafumu ena chifukwa cha anthu akewo. Adati, “Musaŵakhudze odzozedwa anga, musaŵachite choipa aneneri anga.” Imbirani Chauta, inu anthu a dziko lonse lapansi. Lengezani tsiku ndi tsiku za m'mene Iye adapulumutsira anthu ake. Lalikani za ulemerero wake kwa anthu a mitundu yonse, simbani za ntchito zake zodabwitsa kwa anthu a m'maiko onse. Chauta ngwamkulu, ngwoyenera kumtamanda kwambiri, ngwoyenera kumuwopa kupambana milungu yonse. Paja milungu ya anthu a mitundu ina ndi mafano chabe, koma Chauta ndiye adalenga zakumwamba. Ulemerero ndi ufumu zili pamaso pake, mphamvu ndi chimwemwe zili m'Nyumba mwake. Tamandani Chauta, inu anthu a mitundu yonse, vomerezani kuti ulemerero ndi mphamvu, zonse nza Chauta. Tamandani ulemerero wa dzina la Chauta. Bwerani ndi zopereka, ndipo muloŵe m'mabwalo a Nyumba yake. Pembedzani Chauta waulemerero ndi woyera. Njenjemerani pamaso pake, inu anthu onse a pa dziko lapansi. Ndithu dziko lapansi lakhazikika kolimba, osatha kuligwedeza. Zakumwamba zisangalale, za pansi pano zikondwere, zonsezo zilengeze kwa anthu onse kuti, “Chauta ndiye mfumu.” Nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zam'menemo, minda ikondwe pamodzi ndi zonse zomera m'menemo. Mitengo yam'nkhalango idzaimbira Chauta mokondwa, pamene adzabwera kudzalamulira dziko lapansi. Thokozani Chauta, pakuti ngwabwino, chikondi chake chosasinthika nchamuyaya. Munenenso kuti, “Tipulumutseni, Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, mutisonkhanitse ndi kutilanditsa kwa mitundu ina ya anthu, kuti tikuthokozeni potchula dzina lanu loyera, ndi kuti tizinyadira pokutamandani. Atamandike Chauta, Mulungu wa Aisraele, kuyambira muyaya mpaka muyaya!” Tsono anthu onse adati, “Inde momwemo.” Ndipo adatamanda Chauta. Tsono Davide adasiya Asafu pamodzi ndi abale ake kumene kunali Bokosi lachipangano la Chauta, kuti azitumikira nthaŵi zonse ku Bokosilo monga m'mene kunkafunikira tsiku lililonse. Obededomu pamodzi ndi abale ake 68 ankathandizana nawo pa ntchitoyo. Nthaŵi imeneyo Obededomu, mwana wa Yedutuni, ndiponso Hosa, anali ndi udindo wolonda pa makomo. Davide adasiyanso wansembe Zadoki pamodzi ndi abale ake ansembe ku chihema cha Chauta, ku kachisi wa ku Gibiyoni. Adaŵasiya kumeneko kuti azipereka nthaŵi zonse nsembe zopsereza kwa Chauta pa guwa la nsembe zopsereza, m'maŵa ndi madzulo, potsata zonse zimene zidalembedwa m'buku la Malamulo a Mose amene Chauta adalamula Aisraele. Anthuwo anali pamodzi ndi Hemani ndi Yedutuni, kudzanso onse otsala amene adasankhidwa moŵatchula maina, kuti azithokoza Chauta, chifukwa cha chikondi chake chosasinthika ndi chamuyaya. Hemani ndi Yedutuni ankayang'anira malipenga ndi ziwaya zamalipenga, ndiponso zipangizo zina zoimbira nyimbo zachipembedzo. Ana a Yedutuni adaŵaika kuti azilonda pa chipata. Pambuyo pake anthu onse adachoka, aliyense kupita kunyumba kwake. Davide nayenso adapita kwao kuti akadalitse banja lake. Davide atayamba kukhazikika m'nyumba yachifumu, tsiku lina adauza mneneri Natani kuti, “Ine ndikukhala m'nyumba yachifumu yomanga ndi mitengo ya mkungudza, koma Bokosi lachipangano la Chauta likukhala m'hema.” Natani adauza Davide kuti, “Ai, chitani chilichonse chimene mukuganiza mumtima mwanu, poti Mulungu ali nanu.” Koma usiku womwewo Chauta adauza Natani kuti, “Kamuuze mtumiki wanga Davide kuti Ine Chauta ndikuti, Sudzandimangira ndiwe nyumba yoti ndizikhalamo. Ine sindidakhalepo m'nyumba chiyambire tsiku limene ndidatsogolera Aisraele mpaka lero lino. Ndakhala ndikuyenda uku ndi uku ndipo mokhala mwanga munali m'hema. Konse kumene ndakhala ndikuyenda ndi Aisraele onse, kodi ndidaauzapo ndi mmodzi yemwe mwa aweruzi a Aisraele, amene ndidaŵalamula kuti azisunga anthu anga, kuti bwanji sudandimangire nyumba ya mitengo ya mkungudza?” “Nchifukwa chake tsono mtumiki wanga Davide umuuze kuti, ‘Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, Ndidakutenga kubusa kumene unkaŵeta nkhosa kuja, kuti udzakhale mfumu yolamulira anthu anga Aisraele. Ndidakhala nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndidagonjetsa adani ako onse, iweyo ukupenya. Tsono ndidzamveketsa dzina lako, kuti lidzafanefane ndi dzina la anthu otchuka a pa dziko lapansi. Ndipo ndidzaŵasankhira malo anthu anga Aisraele, ndi kuŵakhazika kumeneko, kuti akhale ku malo aoao popanda kuvutikanso. Anthu achiwawa sadzaŵazunzanso monga momwe adaachitira kale lija, kuyambira nthaŵi imene ndidaaika aweruzi a anthu anga Aisraele. Choncho ndidagonjetsa adani ako onse. Kuonjezera pamenepo, ndikukuuza kuti Ine Chauta ndidzakhazikitsa banja lako. Masiku ako atatha kuti ulondole makolo ako kumanda, Ine ndidzakuutsira chiphukira pambuyo pako, mmodzi mwa ana obereka iweyo, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake kolimba. Iyeyo ndiye adzandimangire Nyumba, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake kuti ukhale wamuyaya. Ine ndidzakhala bambo wake, iye adzakhala mwana wanga. Sindidzamchotsera chikondi changa chosasinthika, monga m'mene ndidaachitira ndi Saulo kuti uloŵe ufumu ndiwe. Koma ndidzamkhalitsa mu Nyumba yanga ndi mu ufumu wanga, ndipo ufumu wake udzakhala mpaka muyaya.’ ” Natani adalankhula ndi Davide potsata mau onseŵa, ndiponso potsata zimene adaaziwona m'masomphenyaŵa. Tsono mfumu Davide adaloŵa m'chihema chopembedzeramo Chauta. Adakhala pansi nayamba kupemphera, adati, “Inu Chauta Wamphamvuzonse, ine ndine yani, ndipo banja langa nchiyani, kuti Inu mwandifikitsa mpaka pamene ndiliripa? Komabe zonsezi zinali zazing'ono kwa Inu Mulungu. Mudalankhulanso za banja la ine mtumiki wanu, kulilosera za nthaŵi yaikulu yam'tsogolo. Mwandiwonetsa mibadwo yam'tsogolo, Inu Chauta Mulungu. Ndipo nchiyaninso chimene Davide anganene kwa Inu, popeza kuti mwamchitira ulemu chotere mtumiki wanu? Zoonadi Inu mumamdziŵa mtumiki wanu. Chifukwa chokonda mtumiki wanu, ndiponso malinga ndi mtima wanu, Inu Chauta, mwachita chinthu chachikulu choterechi, pondidziŵitsa zakutsogolozi. Malinga ndi zimene tidamva ndi makutu athu, palibenso wina aliyense wonga Inu Chauta, ndipo palibe mulungu wina koma Inu nokha. Kodi ndi mtundu uti pa dziko lapansi uli wofanafana ndi anthu anu Aisraele, amene Inu Mulungu mudaŵaombola kuti akhale anthu anu? Mudatchuka kwambiri poŵachitira zinthu zazikulu ndi zoopsa, ndiponso popirikitsa mitundu ina ya anthu pamene ankafika anthu anu, amene mudaŵaombola ku Ejipito. Inu mudaŵasandutsa anthu anu Aisraele kuti akhale anthu anu mpaka muyaya, ndipo Inu Chauta mudakhala Mulungu wao. “Tsopano Inu Chauta, musunge mpaka muyaya lonjezo lanu limene mudaachita ponena za ine mtumiki wanu ndi za banja langa, muchite monga momwe mudaanenera. Choncho dzina lanu lidzakhala lomveka mpaka muyaya. Anthu azidzati, ‘Chauta Wamphamvuzonse ndi Mulungu wa Israele, ndiyedi Mulungu wao wa Israele!’ Tsono banja la ine Davide, mtumiki wanu, lidzakhazikika mpaka muyaya. Inu Mulungu mwandiwululira ine mtumiki wanu kuti mudzakhazikitsa banja langa. Nchifukwa chake ine mtumiki wanu ndalimba mtima kuti ndinene pempheroli kwa Inu. Inu Chauta, ndinu Mulungu, ndipo mwalonjeza zinthu zabwino zimenezi kwa mtumiki wanu. Tsono ndikukupemphani kuti mudalitse mokondwa banja la ine mtumiki wanu, likhalebe pamaso panu mpaka muyaya. Pajatu zimene Inu Chauta mwazidalitsa, zimakhala zodalitsidwadi mpaka muyaya.” Pambuyo pake, Davide adathira nkhondo Afilisti naŵagonjetsa. Ndipo adalanda Gati pamodzi ndi midzi yake yomwe kwa Afilistiwo. Adagonjetsanso Amowabu, ndipo Amowabuwo adasanduka otumikira Davide, ndipo ankakhoma msonkho kwa iye. Ku Hamati Davideyo adagonjetsanso Hadadezere mfumu ya ku Zoba, pamene inkapita kukakhazikitsa ulamuliro wake ku mtsinje wa Yufurate. Ndipo Davide adalanda Hadadezere magaleta 1,000, anthu a pa akavalo 7,000, ndi asilikali apansi 20,000. Atatero, Davide adadula mitsempha ya miyendo ya akavalo onse okoka magaleta, koma adasungako akavalo okwanira magaleta 100. Pamene Asiriya a ku Damasiko adaabwera kudzathandiza Hadadezere, mfumu ya ku Zoba, Davide adapha anthu a ku Siriyawo okwanira 22,000. Pambuyo pake Davide adaika maboma a ankhondo ku Damasiko m'dziko la Siriya. Choncho Asiriyawo adasanduka otumikira Davide, nayamba kukhoma msonkho kwa iye. Motero Chauta adampambanitsa Davideyo kulikonse kumene ankapita. Davide adatenga zishango zagolide zimene anyamata a Hadadezere ankanyamula, nabwera nazo ku Yerusalemu. Kuchokera ku Tibati ndi ku Kuni, mizinda ya Hadadezere, Mfumu Davide adabwerako ndi mkuŵa wambiri. Ndi mkuŵa umenewo Solomoni adapanga chimbiya ndi nsanamira ndiponso ziŵiya zina za ku Nyumba ya Chauta. Pamene Tou mfumu ya ku Hamati adamva kuti Davide wagonjetsa gulu lonse la ankhondo la Hadadezere, mfumu ya ku Zoba, adatuma mwana wake Hadoramu kwa mfumu Davide kuti akamlonjere. Adaafunanso kukamuyamika chifukwa chakuti adaamenya nkhondo ndi Hadadezere namgonjetsa. Adaatero pakuti Hadadezereyo ankamenyana nkhondo ndi Tou kaŵirikaŵiri. Tsono adamtumizira Davide mphatso zamitundumitundu zopangidwa ndi golide, siliva ndi mkuŵa. Zimenezonso mfumu Davide adazipereka kwa Chauta, pamodzi ndi siliva ndi golide amene adaafunkha kwa anthu a mitundu ina, ndiye kuti anthu a ku Edomu, a ku Mowabu, kwa Aamoni, kwa Afilisti, ndi kwa Aamaleke. Pa nthaŵi imeneyi Abisai, mwana wa Zeruya, adapha Aedomu okwanira 18,000 ku chigwa cha Mchere. Tsono Davide adaika ankhondo pena ndi pena m'dziko la Edomu, ndipo Aedomu onse adasanduka anthu otumikira Davideyo. Motero Chauta adampambanitsa Davide kulikonse kumene ankapita. Motero Davide adalamulira dziko lonse la Israele, ndipo ankayendetsa zonse mwachilungamo ndi mosakondera. Tsono Yowabu, mwana wa Zeruya, anali mtsogoleri wa ankhondo, ndipo Yehosafati, mwana wa Ahiludi, anali mlembi wolemba mbiri. Zadoki, mwana wa Ahitubi, ndiponso Ahimeleki, mwana wa Abiyatara, anali ansembe, ndipo Savisa anali mlembi. Benaya, mwana wa Yehoyada, anali nduna yoyang'anira Akereti ndi Apeleti. Ndipo ana a Davide anali nduna zazikulu pa ntchito zotumikira mfumu. Pambuyo pake Nahasi, mfumu ya Aamoni, adamwalira, ndipo Hanuni, mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Tsono Davide adati, “Ine ndidzamchitira zabwino Hanuni mwana wa Nahasi, pakuti inenso bambo wake ankandichitira zabwino.” Choncho Davide adatuma amithenga kuti akampepese Hanuni chifukwa cha imfa ya bambo wake. Tsono atumiki a Davidewo adakafika kwa Hanuni, m'dziko la Aamoni, kuti akampepese. Koma akalonga a Aamoni adauza Hanuni kuti, “Kodi mukuganiza kuti m'mene Davide watuma anthu odzakuthuzitsani mtima, ndiye kuti akulemekeza bambo wanu? Osati atumiki akewo abwera kwa inu kuti adzazinde dziko, ndipo kuti akalipenya, alilande?” Choncho Hanuni adagwira atumiki a Davide aja naŵameta ndevu mwachiperengedzu. Kenaka adadula zovala zao pakati mpaka m'chiwuno, naŵabweza kwao. Tsono Davide adamva za atumiki akewo, adatuma anthu kuti akakumane nawo, chifukwa iwowo anali ndi manyazi kwambiri. Ndipo mfumu idati, “Mukaŵauze kuti abakhala ku Yeriko mpaka ndevu zitamera, pambuyo pake ndiye mudzabwere kuno.” Tsono Aamoni atazindikira kuti adziputira mkwiyo wa Davide, Hanuni ndi Aamoniwo adatumiza siliva wa makilogramu 34,000, kuti akalipirire magaleta ndiponso anthu a pa akavalo a ku Mesopotamiya, a ku Aramaaka ndi a ku Zoba. Adalipira magaleta okwanira 32,000, pamodzi ndi mfumu ya ku Maaka ndi gulu lake lankhondo. Amenewo adabwera nadzamanga zithando zankhondo pafupi ndi Medeba. Nawonso Aamoni adabwera kuchokera ku mizinda yao kudzamenya nkhondo. Davide atamva zimenezo, adatuma Yowabu pamodzi ndi gulu lake lonse la ankhondo. Pamenepo Aamoni adatuluka nandanda pa mizere yankhondo pa chipata cha mzinda. Koma mafumu amene adaadzawo anali paokha ku malo opanda mitengo. Yowabu ataona kuti nkhondo yamkhalira kumaso ndi kumbuyo komwe, adasankhula ankhondo amphamvu pakati pa Aisraele naŵandanditsa moyang'anana ndi Asiriyawo. Anthu ena onse otsala adaŵaika m'manja mwa Abisai, mbale wake, ndipo adaŵandanditsa moyang'anana ndi Aamoni. Tsono Yowabu adauza Abisai kuti, “Ngati Asiriya andipose mphamvu, iwe udzandithandize. Koma ngati Aamoni akupose mphamvu, ineyo ndidzabwera kudzakuthandiza. Khala wolimba mtima, ndipo tichite chamuna chifukwa cha anthu athu, ndiponso chifukwa cha mizinda ya Mulungu wathu. Chauta achite zimene zimkomere.” Choncho Yowabu ndi anthu ake adasendera pafupi ndi Asiriyawo kuti amenyane nawo nkhondo, koma Asiriyawo adathaŵa iye akufika. Tsono Aamoni ataona kuti Asiriya athaŵa, nawonso adathaŵa pofika Abisai, mbale wa Yowabu, nakaloŵa mu mzinda. Pamenepo Yowabu adabwerera ku Yerusalemu. Koma Asiriya ataona kuti Aisraele aŵagonjetsa, adatuma amithenga kuti abwere nawo Asiriya anzao amene anali patsidya pa mtsinje wa Yufurate, pamodzi ndi Sofaki mtsogoleri wa ankhondo wa Hadadezere. Davide atamva zimenezi, adasonkhanitsa ankhondo onse a Aisraele, naoloka mtsinje wa Yordani nkukaŵapeza Asiriyawo. Adandanditsa ankhondo ake kuti amenyane nawo. Tsono pamene Davide ankandanditsa ankhondo ake mopenyana ndi Asiriya, iwoŵa adayamba kumenyana naye. Koma pambuyo pake Asiriyawo adathaŵa, kuthaŵa Aisraele. Pamenepo ankhondo a Davide adapha Asiriya okwera magaleta ankhondo okwanira 7,000, ndi ankhondo apansi okwanira 40,000. Adaphanso Sofaki mtsogoleri wa gulu lao lankhondo. Tsono akalonga a Hadadezere ataona kuti Aisraele aŵagonjetsa, adapangana za mtendere ndi Davide, ndipo adayamba kutumikira Aisraelewo. Motero Asiriya sadafunenso kumathandiza Aamoniwo. Itayamba nthaŵi ya phukira chaka chotsatira, nthaŵi imene mafumu ankapita kukamenya nkhondo, Yowabu adatsogolera gulu lankhondo, nakaononga dziko la Aamoni, kenaka adapita kuti akazinge mzinda wa Raba ndi zithando zankhondo. Koma Davide adatsalira ku Yerusalemu. Tsono Yowabu adakantha mzinda wa Raba naugwetsa. Davide adaivula chisoti chagolide mfumu yao, ndipo atachiyesa, adapeza kuti chinkalemera makilogramu 5, ndipo pachisotipo panali mwala wamtengowapatali. Davide adachivala chisoticho, natenga zofunkha zochuluka mumzindamo. Adaŵatulutsa anthu amumzindamo, nakaŵagwiritsa ntchito ndi masowo, zikumbiro zachitsulo ndi nkhwangwa. Umu ndimo m'mene Davide adachitira ndi mizinda yonse ya Aamoni. Pambuyo pake Davideyo adabwerera ku Yerusalemu pamodzi ndi ankhondo onse. Zitapita zimenezi, padauka nkhondo pakati pa Aisraele ndi Afilisti ku Gezere. Tsono Sibekai Muhusati adapha Sipai amene anali mmodzi mwa zidzukulu za ziphona zija zotchedwa Arefaimu, ndipo Afilisti adagonjetsedwa. Kenaka padaukanso nkhondo ndi Afilisti. Tsono Elihanani, mwana wa Yairi, adapha Lami, mbale wa Goliyati Mgiti, amene thunthu la mkondo wake linali lalikulu ngati mtanda woombera nsalu. Panalinso nkhondo ku Gati kumene kunali munthu wina wamtali, wa zala zakumanja uku zisanu ndi chimodzi uku zisanu ndi chimodzi, zakumwendonso uku zisanu nndi chimodzi uku zisanu ndi chimodzi, zonse pamodzi zala 24. Iyeyonso anali mmodzi mwa zidzukulu za Arefaimu. Tsiku lina pamene adanyoza Aisraele, Yonatani, mwana wa Simea, mbale wake wa Davide, adamupha. Anthuwo anali zidzukulu za Arefaimu a ku Gati, ndipo adaphedwa ndi Davide ndi ankhondo ake. Nthaŵi ina Satana adafuna kuvutitsa Aisraele, nanyenga Davide kuti aŵerenge Aisraele. Choncho Davide adauza Yowabu mtsogoleri wa ankhondo kuti, “Pita, ukaŵerenge Aisraele kuyambira ku Beereseba mpaka ku Dani, ndipo udzandiwuze, kuti ndidziŵe chiŵerengero chao.” Koma Yowabu adati, “Chauta achulukitse pa chiwerengero anthu ake makumi khumi kupambana m'mene alirimu. Kodi anthu onseŵa mbuyanga mfumu si atumiki anu? Nanga chifukwa chiyani mbuyanga akufuna zimenezi? Chifukwa chiyani akufuna kuchimwitsa Aisraele?” Koma mfumu idamkakamiza Yowabuyo. Motero Yowabu adachoka nayendera dziko lonse la Israele, pambuyo pake anabwerera ku Yerusalemu. Adapereka chiŵerengero cha anthu onse kwa Davide. Ku dziko lonse la Israele kunali anthu 1,100,000 otha kumenya nkhondo, ndipo ku Yuda kunali 470,000 otha kumenya nkhondo. Koma Yowabuyo sadaphatikizepo dera la Levi ndi la Benjamini poŵerengapo, poti lamulo la mfumulo lidaamuipira. Mulungu nayenso sadakondwere nako kuŵerengako, choncho adaŵakantha Aisraelewo. Pamenepo Davide adayamba kupemphera kwa Mulungu, adati, “Ndachimwa kwambiri ine pazimene ndachitazi. Koma tsopano ndikukupemphani kuti mundikhululukire tchimo langa ine mtumiki wanu, popeza kuti ndachita zopusa kwambiri.” Tsono Chauta adauza Gadi, mneneri wa Davide, kuti, “Pita ukamuuze Davide kuti, Ine Chauta ndikunena kuti, ‘Ndikuika pamaso pako zinthu zitatu zoti ndikuchite. Tsono usankhepo chimodzi ndipo ndidzakuchita.’ ” Gadi adapita kwa Davide nakamuuza kuti, “Chauta akunena kuti, ‘Musankhepo chimene mukufuna: kodi pabwere zaka zitatu za njala, kapena inu mukhale miyezi itatu akukukanthani adani anu namakukugonjetsani pa nkhondo, kapena pagwe mliri wa masiku atatu m'dzikomo pamene Chauta adzakukanthani ndi lupanga, ndipo mngelo wa Chauta adzawononga zinthu m'dziko lonse la Israele.’ Tsono tsimikizani choti ndikamuyankhe amene adanditumayo.” Apo Davide adauza Gadi kuti, “Ine pamenepa ine ndavutika kwambiri mu mtima. Makamaka ndigwe m'manja mwa Chauta, popeza kuti chifundo chake nchachikulu. Koma chonde ndisagwe m'manja mwa anthu ayi.” Motero Chauta adatumiza mliri pa Aisraele, mwakuti adafapo Aisraele okwanira 70,000. Ndipo Mulungu adamtumadi mngelo uja kukaononga Yerusalemu. Koma pamene ankati aziwononga kumene, Chauta adaona namva chisoni, osafunanso kuchita choipacho. Choncho adauza mngelo woonongayo kuti, “Iyai, basi tsopano! Kwakwanira, bweza dzanja lakolo.” Nthaŵi imeneyo nkuti mngelo wa Chauta uja ataima pa malo opunthira tirigu a Orinani Myebusi. Davide adakweza maso ake naona mngelo wa Chautayo ataimirira pakati pa dziko lapansi ndi dziko lakumwamba, m'manja mwake ali ndi lupanga lotambalitsa kuloza ku Yerusalemu. Tsono Davide, pamodzi ndi akuluakulu omwe, atavala ziguduli, adadzigwetsa choŵerama pansi. Ndipo Davide adalankhula ndi Mulungu nati, “Kodi sindine amene ndidalamula kuti akaŵerenge anthu? Ndachimwa ndine, ndipo ndachita choipa. Koma nkhosa izi, kodi zachita chiyani? Inu Chauta Mulungu wanga, dzanja lanu likanthe ine pamodzi ndi banja la bambo wanga. Koma lisati likanthe anthu anuŵa.” Apo mngelo wa Chauta adalamula Gadi kuti, “Kauze Davide kuti akamangire Chauta guwa pa malo opunthira tirigu a Orinani Myebusi uja.” Motero Davide adapita, atamva mau amene Chauta adaalankhula kudzera mwa Gadi. M'menemo nkuti Orinani akupuntha tirigu. Atacheuka adaona mngeloyo, koma ana ake aamuna anai amene anali naye, adaabisala. Pamene Davide adafika kwa Orinani, Orinaniyo adayang'ana, naona Davide, ndipo adatuluka ku malo opunthira tiriguko, nalambira Davide moŵeramitsa nkhope pansi. Davide adauza Orinani kuti, “Undipatse malo opunthira tiriguŵa, kuti ndimangirepo Chauta guwa, kuti mliriwu uŵachoke anthu. Undigulitse pa mtengo wake ndithu.” Tsono Orinani adauza Davide kuti, “Iyai, ingotengani, ndipo mbuyanga mfumu achite zimene zimkomere. Ndikupereka ng'ombe kuti zikhale nsembe yopsereza, mitengo yopunthira kuti ikhale nkhuni, ndiponso tirigu kuti akhale chopereka cha chakudya. Zonsezi ndikuzipereka.” Koma mfumu Davide adauza Orinani kuti, “Iyai, koma ndichita chogula ndi ndalama ndithu pa mtengo wake wathunthu. Sindingatenge chinthu chako kuti ndichipereke kwa Chauta, kupereka ngati nsembe yopsereza chinthu chimene sindidachigule.” Motero Davide adalipira Orinani masekeli agolide 600 chifukwa cha malowo. Ndipo adamangira Chauta guwa kumeneko, napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Adatama Chauta mopemba, ndipo Chautayo adamuyankha potumiza moto wakumwamba, nugwera pa guwa la nsembe zopsereza. Tsono Chauta adalamula mngelo wake, iye nabwezera lupanga m'chimake. Nthaŵi imeneyo Davide ataona kuti Chauta wamuyankha ku malo opunthira tirigu a Orinani Myebusi uja, adapereka nsembe zake kumeneko. Chihema cha Chauta chimene adachipanga Mose kuchipululu kuja ndiponso guwa la nsembe zopsereza, zonsezo zinali ku kachisi wa ku Gibiyoni pa nthaŵi imeneyo. Koma Davide sadathe kupitako kukapempha nzeru kwa Mulungu, poti ankachita mantha ndi lupanga la mngelo wa Chauta uja. Davide adati, “Pano ndipo pamene padzakhale Nyumba ya Mulungu, ndiponso pano mpamene padzakhale guwa la nsembe zopsereza zimene Aisraele azidzapereka.” Davide adalamula kuti asonkhanitse alendo amene anali m'dziko la Israele. Tsono pakati pao adasankhula anthu oti aseme miyala yomangira Nyumba ya Chauta. Davide adaperekanso zitsulo zochuluka zopangira misumali ya zitseko zapamakomo ndi nsimbi zomangira. Adaperekanso mkuŵa wochuluka, wokanika kuuyesa. Adaperekanso matabwa osaŵerengeka a mtengo wa mkungudza, chifukwa anthu a ku Sidoni ndi a ku Tiro adaabwera ndi mikungudza yambiri kwa Davide. Davide ankati, “Mwana wanga Solomoni akali wamng'ono, wosadziŵa zinthu, ndipo nyumba imene akudzamangira Chauta iyenera kukhala nyumba yaulemerero kwambiri, yomveka ndiponso yoyenera kuichitira ulemu anthu a ku maiko onse. Nchifukwa chake ine ndikuti ndikonzeretu zambiri.” Motero Davide adapezeratu zipangizo zambiri asanamwalire. Tsono adaitana Solomoni mwana wake, ndipo adamlamula kuti amangire nyumba Chauta, Mulungu wa Israele. Davide adauza Solomoni kuti, “Mwana wanga, ine ndinkaganiza zakuti ndimangire nyumba Chauta, Mulungu wanga. Koma Chauta adandiwuza kuti, ‘Iwe udapha anthu ambiri ndipo udamenya nkhondo zikuluzikulu. Chifukwa cha zimenezi, sindiwe amene udzandimangire nyumba ai. Udzabereka mwana wamwamuna. Iyeyo adzakhala munthu wamtendere. Ine ndidzamkhalitsa mwamtendere pakati pa adani ake onse omzungulira. Dzina lake adzatchedwa Solomoni, popeza kuti ndidzabweretsa bata ndi mtendere m'dziko lonse la Israele pa moyo wake wonse. Iyeyo ndiye adzandimangire nyumba. Adzakhala mwana wanga, Ine ndidzakhala bambo wake, ndipo ndidzakhazikitsa mpando wake waufumu m'dziko la Israele mpaka muyaya.’ ” Davide adaonjeza kuti, “Tsono mwana wanga, Chauta Mulungu wako akhale nawe, kuti udzathe kummangira nyumba monga m'mene wanenera. Komabe Chauta akuninkhe nzeru ndi luntha, kuti akadzakupatsa ulamuliro woyang'anira Israele, udzasunge malamulo a Chauta Mulungu wako. Ukadzamvera mosamala malamulo ndi malangizo amene Chauta adalamula Mose kuti auze Aisraele, ndiye kuti zinthu zidzakuyendera bwino. Khala wamphamvu, limba mtima, usati uziwopa, usatinso ude nkhaŵa. Movutikira kwambiri ine ndaperekera Nyumba ya Chauta matani 3,400 a golide, matani 34,000 a siliva, ndiponso mkuŵa ndi chitsulo zosadziŵika kulemera kwake, poti zinali zochuluka kwambiri. Ndasonkhanitsanso matabwa ndi miyala. Pa zimenezi uwonjezeponso. Uli nawo anthu antchito ambirimbiri: amisiri a miyala, amisiri a matabwa, ndiponso anthu a nzeru zosiyanasiyana osaŵerengeka, aluso pa ntchito zao za golide, siliva, mkuŵa ndiponso chitsulo. Tiyeko uyambepo ntchito zimenezo. Chauta akhale nawe.” Davide adalamulanso atsogoleri onse a ku Israele kuti azithandizana ndi Solomoni mwana wake, adati, “Pajatu Chauta Mulungu wanu ali nanu, ndipo adakupatsani mtendere ku mbali zonse. Iye wapereka kwa ine nzika zonse zam'dzikomu, mwakuti zagonjera Chauta ndi inu anthu ake. Tsono ikani nzeru zanu ndi mtima wanu pa kutumikira Chauta Mulungu wanu. Muyambepo tsopano kumanga Nyumba ya Chauta kuti muikemo Bokosi lachipangano la Chauta ndiponso ziŵiya zonse zofunikira pa chipembedzo.” Davide atakalamba, masiku ake atatha, adaika Solomoni mwana wake kuti akhale mfumu ya Israele. Davide adasonkhanitsa atsogoleri onse a Israele, ansembe ndi Alevi. Adaŵerenga Aleviwo kuyambira a zaka makumi atatu ndi kupitirirapo. Chiŵerengero chao chinali anthu 38,000. Ndipo adati, “Mwa ameneŵa anthu 24,000 adzakhale oyang'anira ntchito za m'Nyumba ya Chauta. Anthu 6,000 adzakhale nduna ndi aweruzi, anthu 4,000 adzakhale alonda apakhomo, ndipo anthu 4,000 enawo azidzatamanda Chauta ndi zipangizo zoimbira zimene ndazipereka kuti zikhale zotamandira Chauta.” Pambuyo pake Davide adaŵagaŵa anthuwo m'magulumagulu kutsata ana aŵa a Levi: Geresomo, Kohati ndi Merari. Ana a Geresomo anali Ladani ndi Simei. Ana a Ladani anali atatu: Yehiyele mtsogoleri, Zetamu ndi Yowele. Ana a Simei anali atatu: Selomoti, Haziyele ndi Harani. Ameneŵa ndiwo amene anali atsogoleri a mabanja a makolo a Ladani. Ana a Simei anali Yahati, Ziza, Yeusi ndi Beriya. Anai ameneŵa anali ana a Simei. Yahati anali mtsogoleri, ndipo Ziza anali wachiŵiri wake. Koma Yeusi ndi Beriya analibe ana aamuna ambiri, nchifukwa chake adaŵaŵerengera ngati makolo a banja limodzi. Ana a Kohati anali anai: Amuramu, Izara, Hebroni ndi Uziyele. Ana a Amuramu anali Aroni ndi Mose. Aaroni adampatula kuti aziyang'anira zinthu zopatulika za Mulungu. Iyeyo ndi ana ake ankapereka nsembe zofukiza pamaso pa Chauta mpaka muyaya, ndipo ankatumikira ndi kudalitsa anthu m'dzina la Chautayo mpaka muyaya. Koma ana a Mose, munthu wa Mulungu uja, adaŵawerengera pamodzi ndi fuko la Levi. Ana a Mose anali Geresomo ndi Eliyezere. Ana a Geresomo mtsogoleri wao anali Sebuele. Eliyezere anali ndi mwana mmodzi yekha dzina lake Rehabiya. Rehabiyayu anali ndi ana ambirimbiri. Mtsogoleri wa ana a Izara anali Selomiti. Ana a Hebroni naŵa: Yeriya mtsogoleri, wachiŵiri Amariya, wachitatu Yahaziele ndipo wachinai anali Yekameamu. Ana a Uziyele naŵa: Mika mtsogoleri, ndipo wachiŵiri anali Isiya. Ana a Merari naŵa: Mali ndi Musi. Ana a Malai naŵa: Eleazara ndi Kisi. Eleazara adafa opanda ana aamuna, koma aakazi okhaokha. Abale ao, ana a Kisi, ndiwo amene adaŵakwatira. Ana atatu a Musi naŵa: Mali, Edere ndi Yeremoti. Ameneŵa ndiwo amene anali ana a Levi potsata atsogoleri a mabanja a makolo ao, monga m'mene adalembedwera. Ankatsata chiŵerengero cha anthu kuyambira a zaka makumi aŵiri ndi kupitirirapo. Ameneŵa ndiwo amene ankayenera kugwira ntchito yotumikira ku Nyumba ya Chauta. Paja Davide adaati, “Chauta Mulungu wa Israele wapatsa anthu ake mtendere. Ndipo adzakhala ku Yerusalemu mpaka muyaya. Motero nkosafunikiranso kuti Alevi azisenza chihema chija kapena zipangizo za chipembedzo.” Potsata mau omalizira a Davidewo, ameneŵa ndiwo anali chiŵerengero cha Alevi, kuyambira anthu a zaka makumi aŵiri ndi kupitirirapo. “Ntchito yao idzakhala yothandiza ana a Aroni pa ntchito yaunsembe ya ku Nyumba ya Chauta. Azidzasamala mabwalo ndi zipinda, kuyeretsa zonse zimene zili zopatulika, ndiponso azidzagwira ntchito ina iliyonse ya ku Nyumba ya Chauta. Ali nayonso ntchito yosamalira buledi wopatulika, ufa wa nsembe yaufa, mitanda ya buledi wosatupitsa, nsembe zopereka m'chiwaya, nsembe yosanganiza ndi mafuta. Alinso ndi ntchito yoyesa ndi kupima nsembe zonse zoperekedwa m'Nyumba ya Chauta. M'maŵa mulimonse azithokoza ndi kutamanda Chauta. Aziteronso ndi madzulo omwe. Ndipo azitero nthaŵi zonse akamapereka kwa Chauta nsembe zopsereza za masiku a Sabata, za pokhala mwezi uliwonse, ndiponso za pa chikondwerero china chilichonse chachipembedzo. Ntchito zotumikira Chautazi adzazichita kwamuyaya. Motero azidzayang'anira chihema cha msonkhano ndiponso malo opatulika, ndipo azidzathandiza abale ao, zidzukulu za Aroni, potumikira ku chihema chamsonkhano.” Zidzukulu za Aroni ndi izi. Ana a Aroni naŵa: Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara. Koma Nadabu ndi Abihu adafa bambo wao akali moyo, ndipo analibe ana. Motero Eleazara ndi Itamara adaloŵa unsembe. Zidzukulu za Aroni mfumu Davide adazigaŵira ntchito molongosoka bwino, pothandizidwa ndi Zadoki, mmodzi mwa zidzukulu za Eleazara, ndiponso Ahimeleki, mmodzi mwa zidzukulu za Itamara. Popeza kuti pakati pa zidzukulu za Eleazara padapezeka atsogoleri ambiri kupambana pakati pa zidzukulu za Itamara, Davide adasankhula atsogoleri 16 pakati pa zidzukulu za Eleazara, ndiponso asanu ndi atatu pakati pa zidzukulu za Itamara. Adaŵasankhula pochita maere mosakondera, poti panali atumiki a ku Nyumba ya Chauta ndi atsogoleri achipembedzo pakati pa zidzukulu za Eleazara ndiponso pakati pa zidzukulu za Itamara. Magulu aŵiri a zidzukuluzi adachita maerewo motsatana, ndipo mlembi Semaya, mwana wa Netanele, amene anali Mlevi, adalemba maina ao. Mboni zake zinali izi: mfumu, nduna, wansembe Zadoki, Abimeleki mwana wa Abiyatara, ndiponso atsogoleri a mabanja a ansembe ndi a Alevi. Maere oyamba adagwera Yehoyaribu, achiŵiri adagwera Yedaya, achitatu adagwera Harimu, achinai adagwera Seorimu, achisanu adagwera Malikiya, achisanu ndi chimodzi adagwera Miyamini, achisanu ndi chiŵiri adagwera Hakozi, achisanu ndi chitatu adagwera Abiya, achisanu ndi chinai adagwera Yesuwa, achikhumi adagwera Sekaniya, a 11 adagwera Eliyasibu, a 12 adagwera Yakimu, a 13 adagwera Hupa, a 14 adagwera Yesebeabu, a 15 adagwera Biliga, a 16 adagwera Imeri, a 17 adagwera Heziri, a 18 adagwera Hapizeze, a 19 adagwera Petahiya, a 20 adagwera Yehezikele, a 21 adagwera Yakini, a 22 adagwera Gamuli, a 23 adagwera Delaya, a 24 adagwera Maaziya. Ntchito yao ya anthu ameneŵa inali yotumikira m'Nyumba ya Mulungu potsata mwambo umene adaukhazikitsa Aroni kholo lao, monga momwe Chauta Mulungu wa Aisraele adaamlamulira. Atsogoleri ena a mabanja a Levi naŵa: Yedeiya, mdzukulu wa Subaele, amene anali mdzukulu wa Amuramu. Isiya, mdzukulu wa Rehabiya, Yahati, mdzukulu wa Selomoti, amene anali mdzukulu wa Izihara. Ana a Hebroni naŵa: Yeriya mtsogoleri, wachiŵiri Amariya, wachitatu Yahaziele, wachinai Yekameani. Samiri anali mdzukulu wa Mika, kholo lao linali Uziyele. Mbale wake wa Mika anali Isiya. Zekariya anali mdzukulu wa Uziyele, kholo lao linali Isiya. Zidzukulu za Merari nazi: Mali, Musi ndi Yaziya. Adzukulu a Merari, kuchokera mwa Yaziya mwana wake, naŵa: Sohamu, Zakuri ndi Ibiri. Ana a Mali anali aŵa: Eleazara, amene analibe ana, ndiponso Kisi, amene mwana wake anali Yerameele. Ana a Musi anali Mali, Edere ndi Yerimoti. Ameneŵa ndiwo amene anali zidzukulu za Levi potsata mabanja a makolo ao. Mabanja ameneŵanso kuti adziŵe ntchito zao, adachita maere monga abale ao, zidzukulu za Aaroni, akuluakulu ndi ang'onoang'ono omwe. Ochita umboni anali mfumu Davide, Zadoki, Ahimeleki, ndiponso atsogoleri a mabanja a ansembe ndi a Alevi. Davide pamodzi ndi akuluakulu osamalira za utumiki adapatulanso anthu ena otumikira mwa ana a Asafu, a Hemani ndi a Yedutuni amene ankalosa poimba ndi apangwe ndi azeze ndiponso ziwaya zamalipenga. Mndandanda wa anthu amene ankagwira ntchitoyo ndiponso mndandanda wa ntchito zao nawu: Mwa ana a Asafu panali Zakuri, Yosefe, Netaniya ndi Asarela. Amene ankaŵatsogolera ndi Asafu. Ameneŵa ankalalika, mfumu ikaŵalamula kutero Panali ana asanu ndi mmodzi a Yedutuni, maina ao naŵa: Gedaliya, Zeri, Yesaya, Simei, Hasabiya ndi Matitiya. Amene ankaŵatsogolera ndi bambo wao Yedutuni. Iwoŵa ankalalika ndiponso kuimba ndi pangwe pothokoza ndi kutamanda Chauta. Ana a Hemani naŵa: Bukiya, Mataniya, Uziyele, Sebuele, Yerimoti, Hananiya, Hanani, Eliyata, Gidaliti, Romamiti-Yezere, Yosibekasa, Maloti, Hotiri, kudzanso Mahaziyoti. Onseŵa anali ana a Hemani, mneneri wa mfumu, potsata malonjezo a Mulungu akuti adzamkweza iyeyo. Pakuti Mulungu adaampatsa Hemaniyo ana aamuna 14 ndi ana aakazi atatu. Iwowo ankaimba potsata malangizo a bambo wao m'Nyumba ya Mulungu. Ankaimba ndi ziwaya zamalipenga, azeze ndi apangwe potumikira ku Nyumba ya Mulungu. Asafu, Yedutuni ndi Hemani inkaŵalamulira ndi mfumu imene. Anthu onseŵa anali aluso pa zoimba, achibale ao nawonso adaaphunzira kwambiri kuimbira Chauta. Onse pamodzi analipo 288. Poŵagaŵira ntchito zao ankachitira maere, osasiyanitsa pakati pa ang'onoang'ono ndi akuluakulu, aphunzitsi ndi ophunzira. Maere oyamba adagwera Yosefe, wa banja la Asafu. Achiŵiri adagwera Gedaliya, iyeyo ndi abale ake ndi ana ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri. Maere achitatu adagwera Zakuri, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri. Maere achinai adagwera Iziri, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri. Maere achisanu adagwera Netaniya, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri. Maere achisanu ndi chimodzi adagwera Bukiya, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri. Maere achisanu ndi chiŵiri adagwera Yesarela, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri. Maere achisanu ndi chitatu adagwera Yesaya, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri. Maere achisanu ndi chinai adagwera Mataniya, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri. Maere akhumi adagwera Simei, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri. Maere a 11 adagwera Azarele, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri. Maere a 12 adagwera Hasabiya, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri. Maere a 13 adagwera Subaele, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri. Maere a 14 adagwera Matitiya, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri. Maere a 15 adagwera Yeremoti, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri. Maere a 16 adagwera Hananiya, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri. Maere a 17 adagwera Yosibekasa, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri. Maere a 18 adagwera Hanani, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri. Maere a 19 adagwera Maloti, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri. Maere a 20 adagwera Eliyata, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri. Maere a 21 adagwera Hotiri, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri. Maere a 22 adagwera Gidaliti, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri. Maere a 23 adagwera Mahaziyoti, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri. Maere a 24 adagwera Romamiti-Yezere, iyeyo ndi ana ake ndi abale ake, onse pamodzi khumi ndi aŵiri. Magulu a alonda odikira pa khomo naŵa: m'gulu la Akora munali Meselemiya, mwana wa Kore, mmodzi mwa ana a Asafu. Meselemiya anali ndi ana aŵa: wachisamba anali Zekariya, wachiŵiri Yediyale, wachitatu Zebadiya, wachinai Yatiniele, wachisanu Elamu, wachisanu ndi chimodzi Yehohanani ndipo wachisanu ndi chiŵiri Elihunai. Obededomu Mulungu anali ndi ana aŵa: wachisamba anali Semaya, wachiŵiri Yehozabadi, wachitatu Yowa, wachinai Sakara, wachisanu Netanele, wachisanu ndi chimodzi Amiyele, wachisanu ndi chiŵiri Isakara ndipo wachisanu ndi chitatu Peuletai, (pakuti paja Mulungu adaamdalitsa Obededomuyo.) Semaya mwana wake nayenso anali ndi ana amene anali otchuka m'mabanja a makolo ao, makamaka aŵiri omariza. Ana a Semaya naŵa: Otini, Refaele, Obede ndi Elizabadi amene anali ndi abale ao amphamvu, Elihu ndi Semakiya. Kuchokera ku banja la Obededomu kudasankhidwa anthu 62, onsewo okhoza ntchito. Kuchokera ku banja la Meselemiya kudasankhidwa anthu aluso 18. Kuchokera ku banja la Merari kudasankhidwa Hosa amene anali ndi ana aŵa: Simiri mtsogoleri (iyeyu ngakhale sanali mwana wachisamba, atate ake adaamsankhula kuti akhale mtsogoleri.) Wachiŵiri Hilikiya, wachitatu Tebaliya, wachinai anali Zekariya. Onse a m'banja la Hosa amene anali alonda analipo 13. Alonda a pa khomo la Nyumba ya Chauta adaŵaika m'magulu, potsata mabanja ao, ndipo adaŵapatsa ntchito zao zotumikira, monga momwe adachitira Alevi anzao. Iwonso adachita maere pa mabanja onse ang'onoang'ono ndi akuluakulu omwe, kuti apeze okalonda pa makomo. Selemiya adamsankha kuti azilonda pa khomo lakuvuma. Mwana wake Zekariya, phungu wanzeru, adamsankha kuti azilonda khomo lakumpoto. Obededomu adamsankha kuti azilonda khomo lakumwera, ndipo ana ake adaŵaika kuti azilonda nyumba ya katundu. Supimu ndi Hosa adaŵasankha kuti azilonda kuzambwe ku khomo la Saleketi, pa mseu wokwera. Maulonda ankakhala otsatanatsatana. Kuvuma kunkakhala alonda asanu ndi mmodzi tsiku lililonse. Kumpoto kunkakhala alonda anai tsiku lililonse, kumwera alonda anai tsiku lililonse, ndiponso alonda aŵiriaŵiri ku nyumba ya katundu. Ku bwalo lakuzambwe kunali alonda anai ku mseu ndiponso alonda aŵiri ku bwalo lenilenilo. Ameneŵa ndiwo amene anali magulu a alonda apamakomo, ochokera ku mabanja a Akora ndi a Merari. Mwa Alevi, Ahiya ankayang'anira chuma cha ku Nyumba ya Chauta ndiponso zipinda zosungiramo zinthu zopatsidwa kwa Mulungu. Ladani, mmodzi mwa ana a Geresoni, adabereka ana ake amene ankakhala atsogoleri a mabanja, makamaka Ayehiyeli. Ana ena a Ladani, Zetamu ndi Yowele mbale wake, nawonso ankayang'anira chuma cha ku Nyumba ya Chauta. Ena mwa Aamuramu, Aizari, Ahebroni ndi Auziyele adalandira maudindo osiyanasiyana: Sebuele mwana wa Geresomo, mwana wa Mose anali mkulu woyang'anira chuma. Abale ake obadwa mwa Eliyezere anali Rehabiya mwana wake, Yesaiya, Yoramu, Zakiri ndiponso Selomoti. Selomotiyu pamodzi ndi abale ake, ankasunga chuma cha mphatso zopatulika zimene mfumu Davide adazipereka, pamodzi ndi atsogoleri a mabanja, atsogoleri a anthu zikwi, atsogoleri a anthu mazana, ndiponso atsogoleri a magulu a ankhondo. Pa zofunkha zotenga ku nkhondo, adapatulapo mphatso zina kuti zikhale zothandiza kusunga Nyumba ya Chauta. Selomoti pamodzi ndi abale ake, ndiwo amene ankasamalira mphatso zonse zopatulika zoperekedwa ndi mneneri Samuele, ndi Saulo mwana wa Kisi, ndi Abinere mwana wa Nere, ndiponso ndi Yowabu mwana wa Zeruya, ndipo zinthu zina zonse zoperekedwa ndi munthu wina aliyense zinali m'manja mwa Selemoti ndi abale ake. Mwa zidzukulu za Izara, Kenaniya ndi ana ake ndiwo adaŵaika kuti azigwirira Aisraele ntchito zoyang'anira zinthu, monga zolembalemba ndiponso kuweruza milandu. Mwa Ahebroni, Hasabiya pamodzi ndi abale ake 1,700, anthu anzeru, ankayang'anira Aisraele chakuzambwe kwa Yordani, pa ntchito zonse za chipembedzo ndiponso za boma. Yeriya ndiye anali mtsogoleri wa Ahebroni potsata mndandanda wa mabanja a makolo. Pa chaka cha 40 cha ufumu wa Davide padachitika kafukufuku ndipo padapezeka kuti ena otchuka a m'banja la Yeriya ankakhala ku Yazere ku Giliyadi. Mfumu Davide adasankha atsogoleri okwanira 2,700 a m'banja la Yeriyayo kuti aziyang'anira Arubeni, Agadi ndiponso fuko lahafu la Amanase pa zonse zokhudza chipembedzo ndiponso za boma. Nawu mndandanda wa atsogoleri a mabanja a Aisraele olamulira ankhondo zikwi ndiponso ankhondo mazana, pamodzi ndi akulu ao amene ankatumikira mfumu. Ankasinthanasinthana mwezi ndi mwezi pa chaka chilichonse, gulu lililonse linali ndi anthu okwanira 24,000. Yosobeamu mwana wa Zabidiele ankayang'anira gulu loyamba pa mwezi woyamba. Pa gulu lake panali asilikali 24,000. Iyeyu anali mdzukulu wa Perezi, ndipo ndiye anali mkulu wa atsogoleri onse ankhondo mwezi woyamba. Dodai Mwahohi anali woyang'anira gulu la mwezi wachiŵiri. Mtsogoleri wa gulu limeneli anali Mikiloti. Pa gulu lake panali asilikali 24,000. Mtsogoleri wa ankhondo pa mwezi wachitatu anali Benaya, mwana wa Yehoyada mkulu wa ansembe. Pa gulu lake panali asilikali 24,000. Benaya ameneyu ndiye amene ankatsogolera anthu makumi atatu aja. Amizabadi mwana wake ndiye amene ankatsatana naye polamulira gulu lakelo. Asahele, mbale wake wa Yowabu, anali mtsogoleri pa mwezi wachinai, ndipo mwana wake Zebadiya adaloŵa m'malo mwake. Pa gulu lake panali asilikali 24,000. Mtsogoleri pa mwezi wachisanu anali Samuti mdzukulu wa Izara. Pa gulu lake panali asilikali 24,000. Mtsogoleri pa mwezi wachisanu ndi chimodzi anali Ira, mwana wa Ikesi Mtekowa. Pa gulu lake panali asilikali 24,000. Mtsogoleri pa mwezi wa chisanu ndi chiŵiri anali Helezi Mpeloni, mmodzi mwa zidzukulu za Efuremu. Pa gulu lake panali asilikali 24,000. Mtsogoleri pa mwezi wachisanu ndi chitatu anali Sibekai Muhusa, wa m'banja la Zera. Pa gulu lake panali asilikali 24,000. Mtsogoleri pa mwezi wachisanu ndi chinai anali Abiyezere, mmodzi mwa Aanetoti, Mbenjamini. Pa gulu lake panali asilikali 24,000. Mtsogoleri pa mwezi wachikhumi anali Maharai, wa ku Netofa, wa m'banja la Zera. Pa gulu lake panali asilikali 24,000. Mtsogoleri pa mwezi wa 11 anali Benaya wa ku Piratoni, mmodzi wa fuko la Efuremu. Pa gulu lake panali asilikali 24,000. Mtsogoleri pa mwezi wa 12 anali Helidai Mnetofa, mdzukulu wa Otiniyele. Pa gulu lake panali asilikali 24,000. Atsogoleri amene ankayang'anira mafuko a Aisraele anali aŵa: Mtsogoleri wa Arubeni anali Eliyezere, mwana wa Zikiri. Mtsogoleri wa Asimeoni anali Sefatiya, mwana wa Maaka. Mtsogoleri wa Alevi anali Hasabiya, mwana wa Kemuwele. Mtsogoleri wa Aaroni anali Zadoki. Mtsogoleri wa Ayuda anali Elihu, mmodzi mwa abale a Davide. Mtsogoleri wa Aisakara anali Omuri, mwana wa Mikaele. Mtsogoleri wa Azebuloni anali Isimaya, mwana wa Obadiya. Mtsogoleri wa Anafutali anali Yeremoti, mwana wa Aziriele. Mtsogoleri wa Aefuremu anali Hoseya, mwana wa Azaziya. Mtsogoleri wa fuko lahafu la Manase lakuzambwe anali Yowele, mwana wa Pedaya. Mtsogoleri wa fuko lahafu la Manase lakuvuma, dera la Giliyadi anali Ido, mwana wa Zekariya. Mtsogoleri wa Abenjamini anali Yasiyele, mwana wa Abinere. Mtsogoleri wa Adani anali Azarele, mwana wa Yerohamu. Ameneŵa ndiwo amene anali atsogoleri a mafuko a Aisraele. Davide sadaŵerengere kumodzi anthu osafika zaka 20 zakubadwa, pakuti Chauta adaalonjeza kuti Aisraele adzachuluka ngati nyenyezi zakumwamba. Yowabu mwana wa Zeruya adayambapo kuŵerenga, koma sadatsirize ai. Mkwiyo wa Chauta udaŵagwera Aisraele chifukwa cha zimenezi, ndipo chiŵerengerocho sadachiloŵetse m'buku la mbiri ya mfumu Davide. Azimaveti mwana wa Adiyele ankayang'anira chuma cha mfumu. Yonatani mwana wa Uziya ankayang'anira chuma cham'miraga, cham'mizinda, cham'midzi ndi cha m'nyumba zankhondo. Eziri mwana wa Kelubi ankayang'anira anthu ogwira ntchito zolima ku minda. Simei wa ku Rama ankayang'anira minda yamphesa. Zabidi wa ku Sifamu ankayang'anira vinyo kuti asungike bwino mosungira mwake. Baala-Hanani wa ku Gederi anali woyang'anira mitengo ya olivi ndi ya mikuyu ku Sefera. Yowasi ankayang'anira mosungira mafuta. Sitirai wa ku Saroni ankayang'anira ziŵeto za ku busa la ku Saroni. Safati, mwana wa Adilai, ankayang'anira ziŵeto zakuzigwa. Obili Mwismaele ankayang'anira ngamira. Yedeiya Mmeronoti ankayang'anira abulu. Yazizi Muhagiri ankayang'anira nkhosa ndi mbuzi. Onseŵa ndiwo amene anali akulu oyang'anira chuma cha mfumu Davide. Yonatani, mtsibweni wake wa Davide, anali phungu wake, popeza kuti anali munthu womvetsa zinthu, ndiponso wophunzira bwino. Iyeyo pamodzi ndi Yehiyele mwana wa Hakimoni, ankaphunzitsa ana a mfumu. Ahitofele anali phungu wa mfumu, ndipo Husai Mwariki anali bwenzi la mfumu. Ahitofele atamwalira, m'malo mwake mudaloŵa Yehoyada, mwana wa Benaya, ndiponso Abiyatara. Yowabu ndiye anali mtsogoleri wa gulu lankhondo la mfumu. Davide adasonkhanitsa ku Yerusalemu akuluakulu onse a Aisraele, ndiye kuti akuluakulu a mafuko, akapitao a magulu amene ankatumikira mfumu, atsogoleri a ankhondo zikwi, atsogoleri a ankhondo mazana, akulu osunga katundu yense ndi ng'ombe za mfumu ndi za ana ake, pamodzi ndi akulu oyang'anira nyumba ya mfumu, anthu amphamvu, ndiponso ngwazi zonse zankhondo. Tsono mfumu Davide adaimirira nati, “Tamverani abale anga ndiponso anthu anga. Ine ndinkaganiza zomanga nyumba yokhalamo Bokosi lachipangano la Chauta, limene lili ngati malo opondapo mapazi Mulungu wathu. Ndipo ndidakonza zomangira nyumbayo. Koma Mulungu adandiwuza kuti, ‘Iweyo usati undimangire nyumba, poti iwe ndiwe munthu wankhondo ndipo udakhetsa magazi.’ Komabe Chauta, Mulungu wa Israele, adandisankha ine pakati pa onse a m'banja la kholo langa, kuti ndikhale mfumu ya Israele mpaka muyaya. Pajatu Iyeyo adasankha Yuda kuti akhale mtsogoleri wa mafuko onse, ndipo ku fuko la Yuda adasankhako banja la bambo wanga. Ndipo pakati pa ana a atate angawo kudakomera Mulungu kuti asankhe ine, kuti ndikhale mfumu ya Aisraele. Choncho mwa ana anga onse, potitu Chauta adandipatsa ana ambiri, Iyeyo wasankha Solomoni, kuti akhale pa mpando waufumu wa Chauta ndi kumalamulira Israele. Adandiwuza kuti, ‘Solomoni mwana wako ndiye amene adzamange nyumba yanga ndiponso mabwalo anga. Ndamsankha iyeyo kuti akhale mwana wanga, ndipo Ine ndidzakhala bambo wake. Ufumu wake ndidzaukhazikitsa mpaka muyaya, akalimbikiradi kumvera malamulo ndi malangizo anga, monga momwe akuchitira tsopano.’ “Tsono pamaso pa Aisraele onse ndiponso pamaso pa msonkhano umenewu, Mulungu wathu alikumva, ndikukuuzitsani kuti muzisunga ndi kusamala malamulo onse a Chauta Mulungu wanu, kuti mukhalitse m'dziko labwinoli, ndipo lidzakhale nthaŵi zonse choloŵa cha ana anu, inu mutapita. “Ndipo iwe Solomoni mwana wanga, uzimvera Mulungu wa atate ako, ndipo uzimtumikira ndi mtima wonse, modzipereka kwathunthu. Paja Chauta amasanthula mtima wa munthu aliyense, ndipo amadziŵa maganizo a munthu aliyense. Ukamfunafuna, udzampeza. Koma ukalekana naye, Iyeyo adzakutaya mpaka muyaya. Tsono uganizire bwino zimenezi, pakuti Chauta wakusankha iweyo kuti ummangire nyumba, m'mene Iye azikhalamo ngati mwake. Limba mtima tsono, ndipo uigwire ntchitoyi.” Pambuyo pake Davide adapereka kwa Solomoni mwana wake mapulani a Nyumba ya Chauta, oonetsa khonde lake, zipinda zosungiramo chuma, zipinda zake zam'mwamba, zipinda zake zam'kati, ndiponso malo opepesera machimo. Adaperekanso pulani ya zonse zimene ankaziganizira za mabwalo a Nyumba ya Chauta, ya zipinda zonse zozungulira, ya nyumba zosungiramo chuma cha m'Nyumba ya Chauta, ndiponso ya nyumba yosungiramo mphatso zopatulika. Adafotokoza za magaŵidwe a magulu a ansembe ndi a Alevi, ndiponso magaŵidwe a ntchito zonse za m'Nyumba ya Chauta. Adafotokozanso za ziŵiya zonse zogwira nazo ntchito m'Nyumba ya Chauta. Adalangizanso za kulemera kwa golide wopangira ziŵiya zonse zagolide zofunika, kulemera kwa siliva wopangira ziŵiya zasiliva zonse zofunika, kulemera kwa golide wa zoikapo nyale pamodzi ndi nyale zake, kulemera kwa golide wa choikaponyale chilichonse chagolide pamodzi ndi nyale zake, kulemera kwa siliva wa choikaponyale chasiliva pamodzi ndi nyale zake, potsata ntchito ya choikaponyale chilichonse, kulemera kwa golide wa tebulo lililonse la buledi woperekedwa kwa Chauta, kulemera kwa siliva wa matebulo asiliva, kwa golide weniweni wa mafoloko, mabeseni ndi zikho. Adalangizanso za mbale zagolide ndi zasiliva, pamodzi ndi kulemera kwa mbale iliyonse. Adalangiza za kulemera kwa golide wopangira guwa la zofukiza, ndiponso pulani ya guwalo. Adapereka pulani ya galeta lagolide, ndiye kuti akerubi amene ankatambasula mapiko ao kuphimbira Bokosi lachipangano la Chauta. Davide adati, “Zonse ndalembazi zikugwirizana ndi mau amene adalembedwa potsata malangizo a Chauta mwiniwake, ndipo ndidamvetsa bwino kuti ntchito yonseyo iyenera kuchitika potsata mapulaniwo.” Tsono Davide adauza mwana wake Solomoni kuti, “Khala wamphamvu ndipo uchite zimenezo molimba mtima. Usaope, usataye mtima, pakuti Chauta Mulungu wanga ali nawe. Sadzaleka kukusamala ndipo sadzakusiya pa ntchito zonse za Nyumba ya Chautazi. Magulu a ansembe ndi a Alevi oyenera kugwira ntchito zonse za ku Nyumba ya Chauta ngokonzeka ndithu. Ndipo iwe, pa ntchito yonseyo, udzakhala nawo anthu aluso odzipereka pa ntchito yao. Anthu wamba onse ndi atsogoleri ao omwe uzidzaŵalamulira ndiwe zoti achite.” Pambuyo pake Davide adauza msonkhano wonse kuti, “Solomoni mwana wangayu, amene Mulungu yekha wamsankha, akali wamng'ono ndi wosadziŵa zambiri, ndipo ntchitoyi njaikulu. Nyumbayi sidzakhala ya munthu koma ya Chauta. Choncho ndidapereka za ku Nyumba ya Chauta wanga monga m'mene ndidathera, golide wopangira zinthu zagolide, siliva wopangira zinthu zasiliva, mkuŵa wopangira zinthu zamkuŵa, chitsulo chopangira zinthu zazitsulo ndi mitengo yopangira zinthu zamtengo. Ndidaperekanso miyala yochuluka yomangira, ya mtundu wa onikisi, miyala ya maŵangamaŵanga, miyala yambiri yamitundumitundu yamtengowapatali ndiponso miyala ya marabulo. Komanso kuwonjezera pa zonse zimene ndidaperekera Nyumba yoyerayo, ndili nachonso chuma changa cha golide ndi siliva. Ndipo chifukwa cha kudzipereka kwanga pa Nyumba ya Chauta wanga, ndikuchiperekanso chumacho kwa Mulungu wanga. Ndikupereka matani a golide 100, golide wake wabwino kwambiri wa ku Ofiri, ndi matani a siliva wosalala 240. Zonsezo zidzakhala zokutira makoma a Nyumba, ndiponso zogwiritsira ntchito zonse zochitika ndi anthu aluso, golide wopangira zinthu zagolide ndiponso siliva wopangira zinthu zasiliva. Tsono pakati pa inuyonso ndani amene atapeko mwaufulu zinthu zake ndi kuzipereka kwa Chauta?” Pomwepo atsogoleri a mabanja a makolo adapereka zopereka zao mwaufulu, monga momwe adachitiranso atsogoleri a mafuko, atsogoleri a magulu a anthu zikwi, atsogoleri a magulu a anthu mazana ndiponso akapitao a ntchito za mfumu. Zimene adapereka ku ntchito ya Nyumba ya Chauta ndi izi: matani 170 a golide, makilogramu 84 a ndalama zagolide za mtundu wina, matani 340 a siliva, matani pafupifupi 620 a mkuŵa, ndipo matani oposa 3,400 a chitsulo. Aliyense amene anali nayo miyala ya mtengo wapatali, ankaipereka ku nyumba zosungiramo chuma cha Chauta. Amene ankasamala zimenezo anali Yehiyele Mgeresoni. Tsono anthu adakondwa chifukwa chakuti akulu aowo ankapereka mwaufulu ndiponso ndi mtima wao wonse. Nayenso mfumu Davide adakondwa kwambiri. Nchifukwa chake Davide adatamanda Chauta pamaso pa msonkhano wonse. Adati, “Mutamandike mpaka muyaya Inu Chauta, Mulungu wa Israele, kholo lathu. Inu Ambuye, ndinu aakulu, amphamvu, aulemerero, opambana pa nkhondo ndiponso oposa pa ulemu, pakuti zonse zakumwamba ndi za pansi pano nzanu. Mfumu ndinu nokha, Inu Chauta, ndipo wolamulira zonse ndinu. Chuma ndi ulemu zimachokera kwa Inu ndipo mumalamulira zonse, chifukwa muli ndi mphamvu zonse. Inu nokha mutha kukweza munthu ndi kumpatsa mphamvu. Tsopano tikukuthokozani, Inu Mulungu wathu, ndi kutamanda dzina lanu laulemerero. “Koma ine ndine yani, ndipo anthu anga ndi ayani kuti tingathe kupereka mwaufulu motere? Paja zinthu zonse zimachokera kwa Inu ndipo zimene tikupereka kwa Inu nzanu zomwe. Inu Chauta, mukudziŵa kuti ife ndife alendo chabe pansi pano. Tili ngati anthu ongokhala nao chabe, monga momwe analiri makolo athu. Masiku athu okhala pa dziko lapansi ali ngati chithunzithunzi chabe ndipo palibe poti tingakhulupirire. Inu Chauta, Mulungu wathu, inde tapereka mphatso zimenezi kuti akumangireni nyumba, koma zonsezi zikuchokera m'manja mwanu ndipo nzanu zomwe. Mulungu wanga, ndikudziŵa kuti Inu mumapenyetsetsa mtima, ndipo mumakondwera ndi anthu achilungamo. Ndapereka mwaufulu zinthu zonse ndi mtima wolungama, ndipo tsopano ndaŵaona anthu anu amene ali panoŵa nawonso akupereka mwaufulu ndi mokondwa kwa Inu. Inu Chauta, Mulungu wa makolo athu aja, Abrahamu, Isaki ndi Israele, limbitsani nthaŵi zonse maganizo ndi makhalidwe ameneŵa mwa anthu anu, ndipo akhale ndi mtima wokhulupirika mpaka kwa Inu muyaya. Mwana wanga Solomoni mumpatse mtima wangwiro, kuti azisunga malamulo ndi malangizo anu ndi kuŵatsata bwino ndithu, ndiponso kuti amange nyumba imene ine ndaipezera zofunika zonsezi.” Tsono Davide adauza msonkhano wonse kuti, “Tamandani Chauta, Mulungu wanu.” Apo anthu onsewo adatamanda Chauta, Mulungu wa makolo ao. Adaŵeramitsa mitu yao napembedza Chauta, ndipo adalambira mfumu. M'maŵa mwake anthuwo adapereka kwa Chauta, nsembe zopsereza izi: ng'ombe 1,000, nkhosa zamphongo 1,000, ndiponso anaankhosa 1,000, pamodzi ndi chopereka cha chakumwa, kudzanso nsembe zina zochuluka zoperekera Aisraele onse. Tsiku limenelo adadya ndi kumwa mosangalala kwambiri pamaso pa Chauta. Pambuyo pake Solomoni, mwana wa Davide, anthu adamlonga ufumu kachiŵiri. Adamdzoza pamaso pa Chauta kuti akhale mfumu, ndipo Zadokinso kuti akhale wansembe. Tsono Solomoni adakhala pa mpando waufumu wa Chauta nakhala mfumu m'malo mwa Davide atate ake. Zinthu zinkamuyendera bwino, ndipo Aisraele onse ankamumvera. Atsogoleri onse, ankhondo ndi ana a mfumu Davide omwe, onsewo adadzipereka kwa mfumu Solomoni. Aisraele onse adaona m'mene Chauta adakwezera Solomoni. Adampatsadi ukulu wa ufumu wakuti mfumu ina iliyonse sidaulandirepo m'dziko la Israele, iyeyo asanaloŵe. Umu ndimo m'mene Davide, mwana wa Yese, adalamulira Aisraele onse. Nthaŵi imene Davide adalamulira Aisraele idakwanira zaka 40. Adalamulira zaka zisanu ndi ziŵiri ku Hebroni, ndipo ku Yerusalemu adalamulirako zaka 33. Tsono adamwalira atafika pokalamba zedi. Masiku ake adachuluka, pamodzi ndi chuma ndi ulemerero wake. Ndipo Solomoni, mwana wake, adaloŵa ufumu m'malo mwake. Tsono ntchito za mfumu Davide kuyambira pa chiyambi mpaka potsiriza pake, zidalembedwa m'buku la mbiri ya mneneri Samuele, m'buku la mbiri ya mneneri Natani, ndi m'buku la mbiri ya mneneri Gadi. M'menemo adasimba za kulamulira kwake, za mphamvu zake ndiponso za zonse zimene zidamuwonekera iyeyo, mpakanso zimene zidaonekera fuko la Israele ndiponso zimene zidaonekera maiko ena ozungulira. Solomoni mwana wa Davide adakhazikika molimbika mu ufumu wake, ndipo Chauta, Mulungu wake, anali naye, namkweza kwambiri. Solomoni adalankhula ndi Aisraele onse, atsogoleri a anthu zikwi ndiponso atsogoleri a anthu mazana, aweruzi, atsogoleri a Aisraele onse, ndiponso akulu a mabanja. Solomoni pamodzi ndi anthu onse amene adasonkhana nawo, adapita ku kachisi wa ku Gibiyoni. Paja chihema chamsonkhano cha Mulungu chimene Mose, mtumiki wa Chauta, adaamanga ku chipululu chinali kumeneko. (Davide anali atabwera nalo bokosi lachipangano la Chauta kuchokera ku Kiriyati-Yearimu, ndi kulikhazika ku malo amene iye adaakonza, poti adaalimangira hema ku Yerusalemu.) Kuwonjezera pamenepo, guwa lamkuŵa limene adaapanga Bazalele mwana wa Uri, mwana wa Huri, linali komweko kumaso kwa chihema cha Chauta. Ndipo Solomoni adakapembedza kumeneko pamodzi ndi msonkhano wonse. Solomoni adakwera komweko ku guwa lamkuŵa lopembedzerapo Chauta, limene linali ku chihema chamsonkhano, naperekapo nsembe zopsereza zokwanira 1,000. Usiku umenewo Mulungu adamuwonekera Solomoni namuuza kuti, “Upemphe chilichonse chimene ufuna kuti ndikupatse.” Solomoni adati, “Inu Mulungu, mudaonetsa chikondi chanu chachikulu ndi chosasinthika kwa bambo wanga Davide, ndipo tsono mwandiika ine kuti ndikhale mfumu m'malo mwake. Inu Chauta, zimene mudalonjeza kwa bambo wanga Davide zichitikedi, pakuti mwandiika kuti ndikhale mfumu yolamulira anthu ochuluka ngati fumbi la pa dziko lapansi. Tsono mundipatse nzeru ndi luntha, kuti ndiŵatsogolere bwino anthu anuŵa. Nanga popanda nzeruzo ndani angathe kulamulira mtundu waukulu wa anthu anu?” Mulungu adamuyankha kuti, “Chifukwa chakuti waganiza zimenezi mumtima mwako, ndipo sudapemphe katundu, chuma, ulemu, kapena imfa ya adani ako, sudadzipempherenso moyo wautali, koma wapempha nzeru ndi luntha, kuti uzilamulira anthu anga amene ndakulongera ufumu, chabwino nzeruzo ndi luntha ndikupatsa. Ndidzakupatsanso chuma, katundu ndi ulemu, zinthu zoti panalibe ndi mmodzi yemwe amene anali nazo mwa mafumu amene analipo iwe usanabadwe, ndipo sipadzaonekanso wokhala nazo iweyo utafa.” Motero Solomoni adachoka ku kachisi wa ku Gibiyoni pafupi ndi chihema chamsonkhano, nabwera ku Yerusalemu. Ndipo adalamulira Aisraele onse. Adasonkhanitsa magaleta ndiponso anthu okwera pa akavalo. Magaletawo anali nawo 1,400, anthu okwera pa akavalo analipo 12,000. Adaŵakhazika ena ku mizinda yokhalako ankhondo ena pafupi ndi mfumu ku Yerusalemu. Tsono mu Yerusalemumo mfumu idasandutsa siliva ndi golide kukhala wambiri ngati miyala wamba. Adasandutsanso mkungudza kukhala wochuluka ngati mikuyu ya m'zigwa. Solomoni ankagula akavalo ku Ejipito ndi ku Kuwe. Anthu amalonda a mfumu ankalandira akavalowo ku Kuwe, atapereka ndalama. Anthuwo ankagula galeta ku Ejipito pa mtengo wa masekeli asiliva 600 ndipo kavalo pa mtengo wa ndalama zasiliva 150. Momwemonso mafumu onse a Ahiti ndi a ku Siriya nawonso ankagula zinthu kudzera mwa anthu amalonda omwewo. Tsono Solomoni adatsimikiza zoti amange nyumba yopembedzeramo Chauta ndiponso nyumba yaufumu ya iye mwini. Tsono adalemba anthu 70,000 osenza katundu, anthu 80,000 okakumba miyala ku dziko lamapiri, ndiponso akapitao 3,600, oyang'anira anthuwo. Adatumiza mau kwa Hiramu mfumu ya ku Tiro, adati, “Monga momwe munkachitira ndi Davide bambo wanga, pomamtumizira mitengo ya mkungudza, kuti amangire nyumba yake yoti azikhalamo, muchitenso momwemo ndi ine. Ineyo ndikufuna kuti ndimangire nyumba Chauta, Mulungu wanga, ndipo kuti ndiipereke kwa Iye, kuti ikhale yoperekeramo zofukiza za fungo lonunkhira bwino pamaso pa Mulungu, ndi yoperekeramo kosalekeza buledi wopatulika. M'nyumbamo aziperekeramonso nsembe zopsereza m'maŵa ndi madzulo, pa masiku a sabata, pa masiku okhala mwezi ndi pa masiku achikondwerero a Chauta, Mulungu wathu, potsata malamulo okhalira Aisraele mpaka muyaya. Nyumba imene ndimangeyo idzakhala yaikulu, pakuti Mulungu wathu ndi wamkulu kupambana milungu yonse. Koma ndani angathe kummangira nyumba, poti ku mlengalenga ngakhale kumwambamwamba sikungathe kumkwanira Iye? Kodi ine ndinenso yani kuti ndingammangire nyumba, osati kamalo chabe koti nkumafukizapo lubani pamaso pa Mulungu? Tsono tumizireni munthu waluso pa ntchito za golide, siliva, mkuŵa, chitsulo, nsalu yofiirira, yofiira ndi yobiriŵira, ndiponso wodziŵa kuzokota. Akhale pamodzi ndi anthu aluso amene ali ndi ine ku Yuda ndi ku Yerusalemu amene Davide bambo wanga adandipatsa. Munditumizirenso mitengo ya mkungudza, mitengo ya mlombwa ndiponso matabwa ambaŵa a ku Lebanoni, poti ndikudziŵa kuti anyamata anu amadziŵa kudula mitengo ku Lebanoni. Ndipo anyamata anga adzakhala pamodzi ndi anyamata anu, kuti andidulire mitengo yochuluka, popeza kuti nyumba imene ndimangeyo idzakhala yaikulu ndi yochititsa kaso. Anyamata anu odzadula mitengowo ndidzaŵapatsa tirigu wopunthapuntha wokwanira matani 2,000, barele wokwanira matani 2,000, vinyo wa malitara 440,000, ndiponso mafuta a malitara 440,000.” Tsono Hiramu, mfumu ya ku Tiro, adayankha Solomoni pomulembera kalata yonena kuti, “Chifukwa chakuti Chauta amakonda anthu ake, wakuika iweyo kuti ukhale mfumu yao.” Adatinso, “Atamandike Chauta, Mulungu wa Israele, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi, amene adapatsa mfumu Davide mwana wanzeru, waluntha, ndi womvetsa zinthu bwino, woti amange nyumba ya Chauta ndiponso nyumba yaufumu ya iye mwini wake. “Ndatuma mmisiri wanzeru, womvetsa, dzina lake Huramuabi, amene mai wake ndi wa ku Dani, ndipo bambo wake anali wa ku Tiro. Iyeyo ndi wodziŵa bwino ntchito za golide, siliva, mkuŵa, chitsulo, miyala, ndi matabwa, ndiponso nsalu yofiirira, yofiira ndi yobiriŵira, ndiponso bafuta wosalala. Angathe kuchitanso ntchito zonse zozokota, ndi ntchito ina iliyonse imene mungampatse kuti achite pamodzi ndi anthu anu aluso, anthu aluso a mbuyanga Davide bambo wanu. Nchifukwa chake tsono, tirigu, barele, mafuta ndi vinyo zimene mbuyanga wanena, azitumize kwa anyamata antchitowo. Tsono ife tidzadula mtengo uliwonse wa ku Lebanoni umene mungaufune, ndipo tidzakutumizirani mitengoyo poimanga pamodzi ndi kuiyandamitsa pa nyanja mpaka ku Yopa, kuti inuyo muitenge ndi kupita nayo ku Yerusalemu.” Choncho Solomoni adaŵerenga alendo onse amene anali m'dziko lonse la Israele, monga momwe bambo wake Davide adaaŵaŵerengera kale. Ndipo padapezeka anthu okwanira 153,600. Adapatula anthu 70,000 kuti akhale amtengatenga, ndipo anthu 80,000 kuti akhale okumba miyala ku mapiri. Tsono anthu 3,600 adaŵaika kuti akhale akapitao ogwiritsa anthu ntchito. Tsono Solomoni adayambapo kumanga Nyumba ya Chauta ku Yerusalemu pa phiri la Moriya, pamene Chauta adaaonekera Davide bambo wake, pa malo omwe Davide adaaloza, pa bwalo lopunthira tirigu la Orinani Myebusi. Solomoniyo adayamba kumanga pa mwezi wachiŵiri wa chaka chachinai cha ufumu wake. Nyumba ya Chautayo, miyeso yake imene Solomoni adaapereka inali iyi: Potsata miyeso yakale, m'litali mwake inali ya mamita 27, ndipo m'mimba mwake inali ya mamita asanu ndi anai. Chipinda chapoloŵera, m'litali mwake chinali cha mamita asanu ndi anai, kulingana ndi m'mimba mwake mwa nyumbayo. Msinkhu wake unali wa mamita 54. Nyumbayo m'kati mwake adaikuta ndi golide weniweni. Chipinda chachikulucho adachichinga ndi matabwa amlombwa, nachikuta ndi golide wosalala, ndipo pamakoma adalochapo zithunzi za kanjedza ndi za maunyolo. Adaikometsa nyumbayo ndi miyala yamtengowapatali. Golide wake anali wa ku Paravaimu. Motero adaikuta nyumba yonseyo ndi golide, ndiye kuti mitanda yake, ziwundo zake, makoma ake ndi zitseko zake zomwe. Ndipo adazokota zithunzi za akerubi pa makoma. Kenaka adapanga malo opatulika kwambiri. M'litali mwake anali a mamita asanu ndi anai, kulingana ndi m'mimba mwa nyumbayo. M'mimba mwake analinso a mamita asanu ndi anai. Adakuta malo opatulikawo ndi golide wosalala wokwanira matani makumi aŵiri. Magaramu 570 a golide adaŵagwiritsa ntchito kupanga misomali. Ndipo zipinda zapamwamba adazikutanso ndi golide. Ku malo opatulika kwambiriko adapangako akerubi aŵiri achitsulo, ndipo adaŵakuta ndi golide. Mapiko a akerubiwo akaŵatambasula, pamodzi ankakwanira mamita asanu ndi anai. Phiko limodzi la kerubi mmodzi, la mamita aŵiri nkanthu, linkakhudza ku khoma la nyumba. Phiko lake lina, nalonso la mamita aŵiri nkanthu, linkakhudzana ndi phiko la kerubi mnzake. Ndipo Kerubi ameneyu phiko lake limodzi, la mamita aŵiri nkanthu, linkakhudza ku khoma la nyumba, phiko lake lina, nalonso la mamita aŵiri nkanthu, lidalumikizana ndi phiko la kerubi woyamba uja. Mapiko a akerubi amenewo onse pamodzi akaŵatambasula ankakwanira mamita asanu ndi anai. Akerubiwo adaaimirira pa mapazi ao, kuyang'ana m'kati mwa nyumbayo. Ndipo Solomoni adatenga nsalu yobiriŵira, ina yofiira, ina yofiirira, ndi bafuta wosalala, napangira nsalu yochingira, kenaka adapetapo zithunzi za akerubi. Kumaso kwake kwa nyumbayo adamangako nsanamira ziŵiri za msinkhu wa mamita 15 ndi theka. Nsanamira iliyonse inali ndi mutu wa mamita aŵiri nkanthu pamwamba pake. Adapanga maunyolo okometsera, ofanafana ndi aja a m'kati mwa Nyumba ya Chauta, naŵaika pamwamba pa nsanamirazo. Adapanganso zinthu zonga makangaza zokwanira 100, ndipo adaziika ku maunyolowo. Adamanga nsanamirazo kumaso kwa Nyumba ya Chauta, ina chakumwera, ina chakumpoto. Yakumwerayo adaitchula kuti Yakini, yakumpotoyo Bowazi. Solomoni adapanga guwa lamkuŵa, m'litali mwake mamita asanu ndi anai, m'mimba mwake asanu ndi anainso, ndipo msinkhu wake pafupi mamita anai ndi theka. Pambuyo pake adapanga thanki. Thankilo linali loulungika. Pakamwa pake panali pa mamita anai ndi theka, kuyesa modutsa pakati pake. Msinkhu wake unali wa mamita aŵiri nkanthu, ndipo kuzungulira m'thunthu mwake munali mamita 13 ndi theka. M'munsi mwa milomomu adaazokotamo tizikho kuzunguliza thunthu lonse la thankilo, ndiye kuti dera lonse la mamita 13 ndi theka. Tizikhoto tinali m'mizere iŵiri, ndipo adaatipangira kumodzi ndi thankilo pamene ankalipanga. Adalisanjika pa ng'ombe zamkuŵa khumi ndi ziŵiri: zitatu kuyang'ana kumpoto, zitatu kuyang'ana kuzambwe, zitatu kuyang'ana kumwera, zitatu kuyang'ana kuvuma. Thankilo linali litakhazikika pa ng'ombezo, ndipo miyendo yonse yam'munsi ya ng'ombezo idaaloza cham'kati. Thankilo kuchindikira kwake kunali ngati chikhatho. M'milomo mwake munkaoneka ngati m'milomo mwa chikho, ngati duŵa la kakombo. Munkaloŵa madzi okwanira malitara 60,000. Adapanganso mabeseni khumi osambiramo. Kumwera adaikako asanu ndipo kumpoto adaikakonso asanu. M'menemo ndimonso ankatsukiramo zinthu zimene ankagwiritsa ntchito popereka nsembe zopsereza. Koma m'thanki lalikulu lija ndimo m'mene ankasambiramo ansembe. Pambuyo pake adapanga zoikapo nyale khumi zagolide monga momwe kudaalembedwera, ndipo adaziika m'Nyumba ya Chauta, zisanu kumwera, zisanu zina kumpoto. Adapanganso matebulo khumi, ndipo adaŵaika m'Nyumba ya Chauta, asanu kumwera, asanu ena kumpoto. Ndipo adapanga mabeseni agolide okwanira 100. Adapanga bwalo la ansembe, bwalo lalikulu, ndiponso zitseko za bwalo, nazikuta ndi mkuŵa. Ndipo adaika thanki lija pa ndonyo yakumwera ya Nyumbayo. Huramu adapanganso mikhate, mafosholo ndi mabeseni ambiri. Motero Huramu adamatsiriza ntchito ya Nyumba ya Chauta imene ankagwirira mfumu Solomoni: ndiye kuti kumanga nsanamira ziŵiri zija, kupanga makapotolosi aŵiri aja okhala pamwamba pa nsanamirazo, ndiponso maukonde aŵiri aja ophimba ziwaya ziŵiri zija za kunsonga kwa makapotolosi aja okhala pamwamba pa nsanamira. Adapanganso maukonde aŵiri ovundikira pamwamba pa mbale ziŵiri za pa mitu imene inali pamwamba pa nsanamira ija. Adatsirizanso kupanga makangaza 400 amaukonde aŵiri aja, mizere iŵiri ya makangaza pa ukonde uliwonse, kuphimbira ziwaya ziŵiri zija za ku kunsonga kwa makapotolosi okhala pamwamba nsanamira zija. Ndiponso adatsiriza maphaka ndi mbiya zokhala pa maphakawo, thanki lija, ndipo ng'ombe khumi ndi ziŵiri zosanjikapo thankilo. Mikhate, mafosholo, mafoloko ndiponso zipangizo zonse zofunikira pa zimenezi, Huramuabi adazipanga za mkuŵa wonyezemira, kupangira mfumu Solomoni ku Nyumba ya Chauta. Mfumu idapangitsa zimenezi m'chigwa cha Yordani, ku malo amtapo amene ali pakati pa Sukoti ndi Zereda. Solomoni adapangitsa zinthu zimenezo zochuluka kwambiri, kotero kuti kulemera kwa mkuŵawo sikudadziŵike ai. Solomoni adapangitsanso zinthu zonse zimene zinali m'Nyumba ya Mulungu: ndiye kuti guwa lagolide, matebulo a buledi woperekedwa kwa Mulungu. Zoikaponyale pamodzi ndi nyale zake za golide weniweni, kuti ziziyaka m'kati mwenimweni mwa malo opatulika, monga kudaalembedwera. Adapangitsa maluŵa, nyale ndiponso mbano za golide weniweni. Zozimira nyale, mabeseni, mbale zofukiziramo lubani ndiponso ziwaya zopalira moto, zonsezi za golide weniweni. Ndipo adapangitsa zomangira zitseko za Nyumba ya Chauta ija, zitseko zam'kati zoloŵera ku malo opatulika kopambana, ndiponso zitseko zoloŵera m'Nyumba ya Chauta, zonsezo zinali zagolide. Motero Solomoni adatsiriza ntchito zonse za ku Nyumba ya Mulungu. Tsono adabwera ndi zinthu zonse zimene Davide bambo wake adaazipereka, ndipo adaika siliva, golide ndi ziŵiya zonse m'zipinda zosungiramo chuma cha ku Nyumba ya Chauta. Pambuyo pake Solomoni adasonkhanitsa akuluakulu onse a Aisraele, atsogoleri onse a mafuko ndi akuluakulu a mabanja a Aisraele. Onsewo adasonkhana ku Yerusalemu, kuti akatenge Bokosi lachipangano la Chauta, kulichotsa ku Ziyoni, mzinda wa Davide. Aisraele onse adasonkhana pamaso pa mfumu nthaŵi ya chikondwerero cha mwezi wachisanu ndi chiŵiri. Tsono atsogoleri onse a Aisraele atabwera, Alevi adanyamula Bokosi lachipangano lija. Adabwera nalo Bokosilo pamodzi ndi chihema chamsonkhano ndiponso ziŵiya zonse zopatulika zimene zinali m'chihemamo. Ansembe ndi Alevi ndiwo amene adabwera nazo zimenezo. Pamenepo mfumu Solomoni pamodzi ndi gulu lonse la Aisraele amene adaasonkhana pamaso pake, ataima patsogolo pa Bokosi lachipanganolo, ankapereka nsembe za nkhosa ndi ng'ombe zosaŵerengeka. Tsono ansembe adafika nalo Bokosi lachipangano la Chauta lija ku malo ake a m'kati mwenimweni mwa Nyumbayo, ku malo opatulika kopambana naliika kunsi kwa mapiko a akerubi. Choncho akerubiwo ankatambasula mapiko ao pamwamba pa Bokosilo, kotero kuti ankaliphimba pamodzi ndi mphiko zake zonyamulira. Mphikozo zinali zazitali kwambiri, kotero kuti nsonga zake zinkaonekera kukhalira ku malo opatulika kopambana patsogolo pa malo opatulika am'kati mwenimweni. Koma kunja sizinkaonekera. Ndipo zili komweko mpaka pano. M'Bokosimo munalibe kanthu kena kalikonse kupatula miyala iŵiri yokha ija imene Mose adaaikamo ku Horebu, kumene Chauta adaachita chipangano ndi Aisraele, iwowo atatuluka ku Ejipito. Tsono ansembe adatulukamo m'malo opatulikawo (poti ansembe onse amene analipo anali atadziyeretsa, osayang'aniranso magulu ao.) Pamenepo Alevi onse amene ankaimba nyimbo, Asafu, Hemani ndi Yedutuni, ana ao pamodzi ndi abale ao, ovala nsalu za bafuta wambee, ali ndi ziwaya zamalipenga, azeze ndi apangwe, adaimirira cha kuvuma kwa guwa, pamodzi ndi ansembe okwanira 120 amene ankaimba malipenga. Ndipo ntchito ya anthu oimba malipengawo ndi ya anthu oimba nyimbo aja, inali yakuti azimveketsa mau amodzi potamanda ndi kuthokoza Chauta, ndipo ankaimba nyimboyo ndi kuliza malipenga, ziwaya zamalipenga ndiponso zoimbira zina, kutamanda Chauta ndi mau akuti, “Ndithu Chauta ndi wabwino, pakuti chikondi chake chosasinthika chimakhala mpaka muyaya.” Apo Nyumbayo, Nyumba ya Chauta, idadzaza ndi mtambo, ndipo ansembe sankatha kuimirira kuti agwire ntchito yao yotumikira, chifukwa cha mtambowo, pakuti ulemerero wa Chauta unali utadzaza m'Nyumba ya Chautayo. Tsono Solomoni adapemphera nati, “Inu Chauta, mudanena kuti mudzakhala mu mdima waukulu. Ndiye ine ndakumangirani nyumba yaulemerero, malo oti muzikhalamo nthaŵi zonse.” Tsono mfumuyo idatembenukira anthu aja, nidalitsa msonkhano wonse wa Aisraele, onsewo ali chiliri. Ndipo mfumuyo idati, “Atamandike Chauta, Mulungu wa Aisraele, amene wachitadi ndi dzanja lake zimene adaalonjeza ndi pakamwa pake kwa Davide bambo wanga. Paja adaati, ‘Kuyambira tsiku limene ndidatulutsa anthu anga ku Ejipito, sindidasankhepo mzinda pakati pa mafuko onse a Aisraele woti anthu amangemo nyumba m'mene dzina langa lizimvekamo. Ndipo sindidasankhepo munthu woti nkukhala mfumu yomalamulira Aisraele anthu anga. Koma ndidasankha Yerusalemu kuti dzina langa lizimveka kumeneko, ndipo ndidasankha Davide kuti azilamulira anthu anga Aisraele.’ Tsono mumtima mwake bambo wanga Davide ankaganiza zoti amange nyumba yomveketsa dzina la Chauta, Mulungu wa Aisraele. Koma Chautayo adauza Davide bambo wanga kuti, ‘Popeza unkaganiza mumtima mwako zoti undimangire nyumba, udachita bwino kumaganiza zimenezo. Komabe si ndiwe udzamange nyumbayo, koma mwana wako wamwamuna amene udzabale, ndiye amene adzandimangire nyumba yomveketsa dzina langa.’ Tsopano Chauta wachitadi zimene adaalonjeza zija. Pakuti ine ndi amene ndaloŵa ufumu m'malo mwa Davide bambo wanga, ndipo ndikulamulira Aisraele pa mpando wa bambo wanga, monga momwe Chauta adaalonjezera. Ndipo ndinedi amene ndamanga Nyumba yomveketsa dzina la Chauta, Mulungu wa Aisraele. Tsono m'menemo ndaikamo Bokosi lija m'mene muli mau a chipangano cha Chauta chimene adachita ndi Aisraele.” Pambuyo pake Solomoni adaimirira patsogolo pa guwa la Chauta, msonkhano wonse wa Aisraele akuwona, ndipo adatambalitsa manja ake. Iyeyo anali atapanga nsanja yamkuŵa, kutalika kwake mamita aŵiri nkanthu, m'mimba mwake mamita aŵiri nkanthu, msinkhu wake mita limodzi ndi theka, ndipo anali ataimanga m'kati mwenimweni mwa bwalo. Adakwera pansanjapo, ndipo adagwada pa maondo ake, msonkhano wonse wa Aisraele ukuwona, iye anakweza manja ake kumwamba. Tsono adati, “Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, palibe Mulungu wina wonga inu kumwamba kapena pa dziko lapansi. Mumasunga chipangano ndi kuwonetsa chikondi chosasinthika kwa atumiki anu amene amayenda pamaso panu ndi mtima wao wonse. Inu mwachitadi zimene mudaauza Davide bambo wanga, mtumiki wanu. Zimene zija mudaalankhula ndi pakamwa panu, dzanja lanu lazichitadi monga onse akuwoneramu lero lino. Tsono Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, mukumbukire zimene zija mudalonjeza bambo wanga, pamene mudati, ‘Sipadzasoŵa munthu pa banja lako wokhala pamaso panga pa mpando waufumu wa Israele; malinga ana ako akamasamala mkhalidwe wao ndi kumayenda motsata malamulo anga monga momwe iweyo wayendera pamaso panga.’ Nchifukwa chake tsono, Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, zimene mudalankhula ndi Davide mtumiki wanu zichitikedi. “Kodi Mulungu angakhale nawodi anthu pa dziko lapansi? Onani kumwamba ndi kumwambamwamba komwe sikukukwanirani kukhala, nanji tsono nyumba imene ndakumangiraniyi. Komabe Inu Chauta, Mulungu wanga imvani pemphero la ine mtumiki wanu ndi kupemba kwanga. Mverani kulira kwanga ndiponso pemphero limene ine, mtumiki wanu ndikupemphera pamaso panu. Usana ndi usiku maso anu azikhala otsekuka, kuyang'ana Nyumba imeneyi, malo amene Inu mudanena kuti mudzamveketsamo dzina lanu. Imvani pemphero limene mtumiki wanu akupemphera ku malo ano. Muzimva mapemphero opemba a mtumiki wanu ndiponso a anthu anu Aisraele, akamapemphera ku malo ano. Ndithu mumve kumwambako kumene mumakhala, ndipo mukamva, mutikhululukire. “Tsono munthu akachimwira mnzake, nauzidwa kuti alumbire, akabwera kudzalumbira patsogolo pa guwa lanu m'Nyumba muno, pamenepo Inu mumve kumwambako, ndipo muchitepo kanthu ndi kuŵaweruza atumiki anuwo. Wochimwa mugamule kuti ngwolakwa ndipo mumlange chifukwa cha zolakwa zakezo. Koma wosachimwayo mugamule kuti ngwopanda mlandu, ndipo mumpatse mphotho molingana ndi makhalidwe akewo. “Anthu anu Aisraele atagonjetsedwa ndi adani ao chifukwa chakuti adakuchimwirani, pambuyo pake nkutembenuka ndi kutamanda dzina lanu, napemphera ndi kupemba kwa Inu okhala m'Nyumba muno, pamenepo Inuyo mumve kumwambako, ndipo mukhululukire tchimo la anthu anu Aisraele. Kenaka muŵabwezenso ku dziko limene Inu mudaŵapatsa iwowo ndi makolo ao. “Kumwamba kukatsekeka, mvula nkupanda kugwa, chifukwa chakuti anthuwo adakuchimwirani, pambuyo pake nkupemphera choyang'ana ku malo ano ndi kutamanda dzina lanu, natembenuka nkusiya tchimo laolo Inu mukuŵazunza, pamenepo Inuyo mumve kumwambako, mukhululukire tchimo la atumiki anu, anthu anu Aisraele. Inu muziŵaphunzitsa njira yabwino yoti aziyendamo, ndipo muzigwetsa mvula pa dziko lanu limene mudapatsa anthu anu kuti likhale choloŵa chao. “Mwina mwake m'dzikomo mudzaloŵa njala, mliri, dzimbiri lapambeu kapena chinoni, dzombe kapena kapuchi. Mwina adani ao adzaŵazinga ku mzinda wao wina uliwonse. Mwina padzakhala mliri wamtundu wina kapena matenda a mtundu uliwonse. Tsono, chodandaula kapena chopembera chingakhale chotani, pempherolo lingakhale la munthu m'modzi kapena la anthu anu onse Aisraele wina aliyense akapemphera mopemba, akuzindikira zovuta za mumtima mwake, natambalitsa manja choloza ku Nyumba ino, pamenepo Inuyo mumve kumwambako kumene mumakhala. Mukhululuke ndipo muchitepo kanthu. Muchitire aliyense potsata makhalidwe ake onse pakuti Inu mukudziŵa mtima wake. Inu nokha ndinu amene mumadziŵa mitima ya anthu. Motero anthuwo azikuopani ndi kumayenda m'njira zanu masiku onse a moyo wao pomakhala m'dziko limene Inu mudapatsa makolo athu. “Chimodzimodzinso mwina mlendo amene sali mmodzi wa Aisraele anthu anu, adzabwera kuchokera ku dziko lakutali, atamva za dzina lanu lotchuka ndiponso dzanja lanu lamphamvu ndi lochita zazikulu. Iyeyo akadzabwera kudzapemphera ku Nyumba ino, Inu mumve kumwambako kumene mumakhala, ndipo mumchite mlendoyo zonse zimene wakupemphani. Muchite zimenezi kuti anthu onse a pa dziko lapansi adziŵe dzina lanu, ndipo azikumverani monga m'mene amachitira Aisraele anthu anu, ndipo adziŵe kuti Nyumba imene ndaimangayi imadziŵika ndi dzina lanu. “Anthu anu akamapita ku nkhondo kukamenyana ndi adani ao, kulikonse kumene mungaŵatume, akapemphera kwa Inu choyang'ana ku mzinda uno umene Inu mudausankha, ndiponso ku Nyumba imene ndakumangiraniyi yomveketsa dzina lanu, pamenepo Inuyo mumve kumwambako pemphero lao ndi kupemba kwao, ndipo muŵapambanitse. “Mwina anthuwo adzakuchimwirani, poti palibe munthu amene sachimwa, ndiye Inuyo nkudzaŵakwiyira ndi kuŵapereka kwa adani, kuti aŵatenge ukapolo kupita nawo ku dziko lakutali kapena lakufupi. Tsono, ali akapolo kuchilendoko akazindikira kuchimwa kwao natembenuka mtima ndi kupemphera kwa Inu modzichepetsa m'dziko laukapololo nkumanena kuti, ‘Tachimwa, tachita zosayenera, tapalamula ndithu,’ anthuwo akabwerera kwa Inu ndi maganizo ao onse ndi mtima wao wonse, m'dziko laukapolo kumene iwo aja adaŵatengera, ndipo akapemphera choloza ku dziko lao limene Inu mudapatsa makolo ao, ku mzinda umene Inu mudausankha, ndiponso ku Nyumba imene ine ndakumangiraniyi yomveketsa dzina lanu, pamenepo Inuyo kumwambako, kumene mumakhala, mumve pemphero lao ndi kupemba kwao. Muŵachitire zolungama, ndipo muŵakhululukire anthu anu okuchimwiraniwo. Tsopano, Inu Mulungu wanga, tsekulani maso anu, ndipo makutu anu amve pemphero ili la ku malo ano. “Inu Chauta, dzambatukani tsopano, mupite ku malo anu kumene mumapumulako, Inuyo ndi bokosi la mphamvu zanu. Inu Chauta, ansembe anu avale chilungamo, anthu okutumikirani akondwe nazo zabwino zanu. Inu Chauta musati mumfulatire wodzozedwa wanu. Kumbukirani chikondi chanu chosasinthika kwa mtumiki wanu Davide.” Solomoni atatha kupemphera, moto udatsika kuchokera kumwamba, nuwotcha nsembe zopsereza pamodzi ndi nsembe zina. Pomwepo ulemerero wa Chauta udadzaza Nyumba ya Chauta ija. Tsono ansembe sadathe kuloŵa m'Nyumbamo, popeza kuti ulemerero wa Chauta unali utadzaza m'menemo. Ndipo Aisraele onse ataona moto wotsika kumwambawo, pamodzi ndi ulemerero wa Chauta m'Nyumba ya Chauta ija, adaŵerama, nazyolikitsa nkhope zao pansi, ndipo adapembedza nathokoza Chauta ndi mau akuti, “Ndithu Chauta ndi wabwino pakuti chikondi chake chosasinthika chimakhala mpaka muyaya.” Tsono mfumu pamodzi ndi anthu onsewo adapereka nsembe pamaso pa Chauta. Mfumu Solomoni adapereka nsembe pakupha ng'ombe 22,000 ndi nkhosa 120,000. Motero mfumuyo pamodzi ndi anthu onsewo adaipereka Nyumba ya Mulungu ija. Ansembe adaimirira m'malo mwao, pamene Alevi ankatamanda Chauta poimba nyimbo zothokoza Chauta ndi zipangizo zimene Davide adapanga, pakuti chikondi cha Mulungu chimakhala mpaka muyaya. Anthu onseŵa ankatero nthaŵi zonse Davide akamapereka matamando kudzera mwa iwo. Poyang'anana ndi iwowo panali ansembe oliza malipenga. Ndipo Aisraele onse adaakhala chilili. Tsono Solomoni adapatula malo apakatikati a bwalo lija lokhala kumaso kwa Nyumba ya Chauta, ndipo kumeneko adaperekako nsembe zopsereza ndiponso mafuta a nsembe zachiyanjano, chifukwa chakuti pa guwa lamkuŵa limene adapanga Solomoni lija, panalibe malo oti nkukhalapo nsembe zonse zopsereza ndi zopereka za chakudya, pamodzi ndi mafuta omwe. Nthaŵi imeneyo Solomoni adachita chikondwerero cha masiku asanu ndi aŵiri pamodzi ndi Aisraele onse. Unali msonkhano waukulu kwambiri, kuyambira ku chipata cha ku Hamati mpaka ku kamtsinje wa ku Ejipito. Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu adachita mwambo wotsekera. Pakuti masiku asanu ndi aŵiri anthuwo ankachita mwambo wopereka guwa, ndipo masiku ena asanu ndi aŵiri kunali chikondwerero. Pa tsiku la 23 la mwezi wachisanu ndi chiŵiriwo, Solomoni adauza anthu aja kuti apite kwao. Anthuwo anali okondwa ndiponso a mtima wosangalala, chifukwa cha zokoma zimene Chauta adaachitira Davide ndi Solomoni ndiponso Aisraele, anthu ake. Motero Solomoni adamaliza kumanga Nyumba ya Chauta ndi nyumba ya mfumu ndipo zonse zimene adaaganiza kuti achite m'Nyumba ya Mulungu ndi m'nyumba yake adazimalizadi mokhoza kwambiri. Tsono Chauta adamuwonekera usiku namuuza kuti, “Ndamva pemphero lako, ndipo ndadzisankhira malo ano kuti akhale Nyumba yoperekera nsembe. Ndikatseka kumwamba kuti mvula isagwe, kapena ndikalamula dzombe kuti liwononge zomera zapadziko, kapena ndikatumiza mliri pakati pa anthu anga, ndipo anthu anga amene amatchedwa dzina langa akadzichepetsa, napemphera, ndi kufunafuna nkhope yanga, nasiya njira zao zoipa, pamenepo Ine ndidzamva kumwambako. Choncho ndidzaŵakhululukira zoipa zao ndi kupulumutsa dziko lao. Ndiye maso anga adzatsekuka, ndipo ndidzatchera khutu ku pemphero limene adzapemphere ku malo ano. Chifukwa tsopano ndaisankha ndipo ndapatula Nyumba ino kuti dzina langa lizikhala m'menemo mpaka muyaya. Maso anga ndi mtima wanga, zidzakhala m'menemo nthaŵi zonse. Tsono iweyo ukamayenda pamaso panga monga m'mene ankayendera Davide bambo wako, ukamachita zonse zimene ndidakulamula ndi kumvera mau anga ndi malangizo anga, ukatero Ine ndidzaukhazikitsa mpando wako waufumu, monga momwe ndidalonjezera Davide bambo wako kuti, ‘Sipadzasoŵa munthu pa banja lako wolamulira Israele.’ “Koma inu mukapatuka ndi kusiya malamulo anga ndi malangizo anga amene ndidakupatsani, mukamatumikira milungu ina ndi kumaipembedza, pamenepo ndidzaŵachotsa Aisraelewo m'dziko limene ndidaŵapatsa. Ndipo nyumba ino imene ndaipatulira dzina langa, ndidzaichotsa pamaso panga, ndipo ndidzaisandutsa ngati mwambi ndi chisudzo chabe pakati pa anthu a mitundu yonse. Ndiye Nyumba yotchuka ndi yokomayi, aliyense wopitapo adzadabwa nadzafunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani Chauta walichita zotere dzikoli, ndiponso Nyumbayi?’ Tsono azidzati, ‘Nchifukwa chakuti anthuwo adasiya Chauta, Mulungu wa makolo ao, amene adaŵatulutsa ku dziko la Ejipito, ndipo adadzifunira milungu ina, namaipembedza ndi kumaitumikira. Nkuwona Chautayo waŵachita zoipa zonsezi.’ ” Ntchito yomanga Nyumba ya Chauta ndi nyumba ya mfumu idamtengera Solomoni zaka makumi aŵiri. Pambuyo pake adamanganso kachiŵiri mizinda imene Huramu adampatsa, nakhazikamo Aisraele. Kenaka Solomoni adapita ku Hamatizoba nakaulanda mzindawo. Adakamanga Tadimori ku chipululu, ndiponso mizinda yosungirako chuma, imene adakaimanga ku Hamati. Adamanganso Betehoroni wakumtunda ndi Betehoroni wakunsi, mizinda yamalinga yokhala ndi makoma, zitseko ndi mipiringidzo. Adamanganso Baalati ndiponso mizinda yonse yosungiramo zinthu zimene anali nazo, mizinda yonse yosungiramo magaleta ake, ndi ina yomakhalamo anthu ake okwera pa akavalo, ndi zonse zimene Solomoni adafuna kuti amange ku Yerusalemu, ku Lebanoni ndi ku madera onse amene Solomoni ankaŵalamulira. Koma analipo anthu ena otsalira a mitundu yosiyanasiyana: Ahiti, Aamori, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. Ameneŵa sanali Aisraele, ndiye kuti zidzukulu zao zidaatsalira m'dzikomo, Aisraele ataloŵamo. Onsewo Aisraele sadaŵaononge. Anthu ameneŵa Solomoni ankaŵagwiritsa ntchito yathangata. Ndipo akugwirabe ntchito imeneyo mpaka lero lino. Koma Aisraele Solomoni sankaŵagwiritsa ntchito yaukapolo. Iwowo anali anthu ake ankhondo, nduna zake, oyang'anira magaleta ake ndi anthu ake okwera pa akavalo. Ndipo akuluakulu a mfumu Solomoni analipo 250 amene ankalamulira anthu. Solomoni adatenga mwana wamkazi wa Farao ku mzinda wa Davide, nabwera naye ku nyumba imene adamangira mkaziyo, poti Solomoniyo ankati, “Mkazi wanga asamakhale m'nyumba ya Davide mfumu ya Israele, chifukwa chakuti malo amene kwafikira Bokosi lachipangano la Chauta ngopatulika.” Kenaka Solomoni adapereka nsembe zopsereza kwa Chauta pa guwa la Chauta limene adalimanga patsogolo pa khonde lapoloŵera, monga momwe zinkafunikira pa tsiku lililonse. Ankapereka potsata malamulo a Mose okhudza masiku a Sabata, masiku a pokhala mwezi watsopano, ndiponso masiku achikondwerero atatu a chaka ndi chaka: Chikondwerero cha buledi wosafufumitsa, chikondwerero cha masabata ndiponso chikondwerero cha mahema. Potsata malangizo a Davide bambo wake, adagaŵa ansembe m'magulumagulu ndi kuŵapatsa ntchito zao. Adaikanso magulu a Alevi ndi kuŵapatsa ntchito yao yoimba nyimbo zotamanda Mulungu ndi yotumikira ansembe, monga momwe ntchito ya tsiku lililonse inkafunikira. Magulu a alonda apazipata adaŵagaŵira udindo wao pa chipata chilichonse. Paja Davide, munthu wa Mulungu, anali atalamula motero. Ndipo anthu sadapatukepo pa zimene mfumu idaalamula ansembe ndi Alevi, zokhudza zinthu zonsezi ndiponso zokhudza nyumba zosungiramo chuma. Motero ntchito zonse za Solomoni zidatha, kuyambira pamene maziko a Nyumba ya Chauta adaikidwa mpaka pamene ntchitoyo idatha. Choncho Nyumba ya Chauta idatheratu. Pambuyo pake Solomoni adapita ku Eziyoni-Gebere ndi ku Elati kumphepete kwa nyanja, ku dziko la Edomu. Tsono mfumu Hiramu adamtumizira zombo ndi anyamata ake amene ankadziŵa za zapanyanja. Anthuwo adapita ku Ofiri, pamodzi ndi anyamata a Solomoni, ndipo adakatengako golide wa makilogramu 18,000, nabwera naye kwa mfumu Solomoni. Mfumukazi ya ku Sheba itamva za mbiri ya Solomoni, idadza ku Yerusalemu kudzamuyesa ndi mafunso apatali. Idabwera ndi atumiki ambiri ndi ngamira zonyamula zokometsera zakudya, golide wambiri ndi miyala yamtengowapatali. Itafika kwa Solomoni, idamuuza zonse za kumtima mwake. Solomoni adayankha mafunso ake onse. Panalibe kanthu kalikonse kobisika kwa Solomoniyo, kamene sadathe kuimasulira mfumukaziyo. Tsono itaona nzeru zonse za Solomoni, nyumba imene adaamanga ija, chakudya cha patebulo pake, m'mene zinkakhalira nduna zake, m'mene ankasungira mwambo atumiki ake ndi zovala zao, atumiki ake operekera zakumwa ndi zovala zao, ndiponso nsembe zake zopsereza zimene ankapereka ku Nyumba ya Chauta, mfumukaziyo idangoti kukamwa pululu, kusoŵa chonena. Pamenepo idauza mfumu Solomoni kuti, “Zimene ndinkamva ndili kudziko la kwathu zonena za ntchito zanu ndi nzeru zanu, nzoonadi. Zimenezo sindidazikhulupirire, mpaka nditafika ndikuona chamaso. Ndipotu anthu sadaandiuzeko zonse ngakhale ndi theka lomwe la nzeru zanu zonse. Mukupambana kutali mbiri imene ndidaaimva. Ngodala anthu anu. Ngodala atumiki anuŵa, amene amaima pamaso panu nthaŵi zonse nkumamva nzeru zanu. Atamandike Chauta, Mulungu wanu, amene wakondwera nanu, nakukhazikani pa mpando wake waufumu, kuti mukhale mfumu yotumikira Chauta, Mulungu wanu. Mulungu adakulongani ufumu kuti muzilamulira Aisraele, chifukwa choti Mulungu wanu adakonda Israele mpaka muyaya, nafuna kuti akhalepo mpaka muyaya, wakuikani kuti mukhale mfumu yake yolamulira moyenera ndi mwachilungamo.” Itanena zimenezo mfumukaziyo idapatsa mfumu Solomoni golide wa makilogramu 4,000, zonunkhira zambirimbiri ndiponso miyala yamtengowapatali. Nkale lonse sikudaoneke zokometsera chakudya zonga zimene mfumukazi ya ku Sheba idapatsa mfumu Solomoni. Komanso anyamata a mfumu Hiramu pamodzi ndi anyamata a Solomoni amene adaabwera ndi golide wa ku Ofiri, adabweranso ndi mitengo ya mbawa ndi miyala yamtengowapatali. Ndipo mitengo ya mbawayo mfumu idasanjira makwerero a ku Nyumba ya Chauta ndi a ku nyumba ya mfumu. Ndipo anthu oimba nyimbo adaŵapangira apangwe ndi azeze, amene kunalibe nkale lonse ku dziko la Yuda. Tsono Solomoni adapatsa mfumukazi ya ku Sheba ija zonse zimene inkafuna ndiponso chilichonse chimene idaapempha, osaŵerengera zimene anali ataipatsa kale posinthana nayo mphatso. Tsono mfumukaziyo idabwerera ku dziko lakwao pamodzi ndi atumiki ake aja. Golide amene ankabwera kwa Solomoni pa chaka chimodzi ankakwanira makilogramu 23,000, osaŵerengera amene ankabwera ndi anthu amalonda. Mafumu onse a ku Arabiya pamodzi ndi nduna zam'dzikomo ankabwera ndi siliva ndi golide kwa Solomoni. Mfumu Solomoni adapangitsa zishango 200 zazikulu za golide wonsansantha. M'chishango chilichonse munkaloŵa golide pafupi makilogramu pafupi asanu ndi aŵiri. Adapanganso zishango 300 zazing'ono za golide wonsansantha. M'chishango chilichonse munkaloŵa golide wokwanira makilogramu atatu. Tsono mfumu idaika zishangozo m'Nyumba ya Nkhalango ya ku Lebanoni. Mfumu idapangitsanso mpando waukulu waufumu wa minyanga yanjovu niwukuta ndi golide weniweni. Mpando waufumuwo unali ndi makwerero asanu ndi limodzi okafikirapo, ndiponso chopondapo mapazi, zonsezo zagolide. Mpandowo unali ndi zogwirira ndi zosanjikapo manja uku ndi uku, ndiponso zifanizo ziŵiri za mikango iŵiri itaima pambali pa zosamizapo manjazo. Panalinso mikango pa mbali zonse ziŵiri za kwerero lililonse, mikango khumi ndi iŵiri yonse pamodzi. Mpando sudapezekepo mu ufumu wina uliwonse. Zikho zonse zimene mfumu Solomoni ankamwera zinali zopangidwa ndi golide, ziŵiya zonse za ku Nyumba ya Nkhalango ya ku Lebanoni nazonso zinali za golide weniweni. Siliva sanalinso kanthu pa nthaŵi ya Solomoni. Mfumu inali ndi zombo zimene zinkapita ku Tarisisi ndi anyamata a mfumu Huramu, ndipo chaka chachitatu chilichonse, zombo za ku Tarisisi zinkabwera ndi golide, siliva, minyanga yanjovu, anyani ndi apusi. Motero mfumu Solomoni adapambana mafumu onse a pa dziko lonse lapansi pa chuma ndi pa nzeru. Ndipo mafumu onse a pa dziko lapansi ankafunafuna kuti amuone Solomoni ndi kumva nzeru zake zimene Mulungu adaaika mumtima mwake. Aliyense mwa iwo ankabwera ndi mphatso zake, zinthu zasiliva ndi zagolide, zovala, zida zankhondo, zokometsera chakudya, akavalo ndi abulu. Ndipo zimenezi zinkachitika choncho chaka ndi chaka. Solomoni anali ndi zipinda 4,000 zosungiramo akavalo ndi magaleta ake, ndiponso anthu 12,000 okwera pa akavalo. Adaŵaika ena ku mizinda yokhalako ankhondo, ena pafupi ndi mfumu ku Yerusalemu. Tsono ankalamulira mafumu onse kuyambira ku Yufurate mpaka ku dziko la Afilisti, mpakanso ku malire a ku Ejipito. Ndipo ku Yerusalemu mfumuyo idasandutsa siliva kukhala wambiri ngati miyala wamba. Adasandutsanso mikungudza kukhala wochuluka ngati mikuyu ya m'zigwa. Akavalo ankaŵaitanitsa ku Ejipito ndi ku maiko onse, kugulira Solomoni. Tsono ntchito zina zonse za Solomoni kuyambira pa chiyambi mpaka kumaliza, paja zidalembedwa m'buku la mbiri ya mneneri Natani, ndi m'buku la ulosi wa Ahiya wa ku Siloni, ndiponso m'buku lokamba zimene mneneri Ido adaziwona m'masomphenya zokhudza Yerobowamu mwana wa Nebati. Solomoni adalamulira Aisraele onse ku Yerusalemu zaka makumi anai. Ndipo adamwalira, naikidwa m'manda mu mzinda wa Davide bambo wake. Ndipo Rehobowamu, mwana wake, adaloŵa ufumu m'malo mwake. Tsono Rehobowamu adapita ku Sekemu. Apo nkuti Aisraele onse atapita kale ku Sekemuko, kuti akamulonge ufumu. Nthaŵi imeneyo nkuti Yerobowamu, mwana wa Nebati, ali ku Ejipito, momwe adaathaŵira mfumu Solomoni muja. Tsono atamva zaufumuzo, adachokako ku Ejipito. Anthu adakamuitana. Choncho Yerobowamu pamodzi ndi Aisraele onse, adadza kwa Rehobowamu namuuza kuti, “Bambo wanu ankatisenzetsa goli lolemetsa kwambiri. Ndiye ife tikuti inu tsopano mudzatipeputsireko goli lolemetsalo ndi ntchito zoŵaŵa zimene bambo wanu adatisenzetsa, apo ife tidzakutumikirani.” Rehobowamu adaŵauza kuti, “Mukabwerenso kuno patapita masiku atatu.” Choncho anthuwo adachoka. Tsono mfumu Rehobowamu adapempha nzeru kwa madoda amene ankakhala ndi bambo wake Solomoni ndi kumamlangiza akali moyo. Adaŵafunsa kuti, “Inu mungandilangize zotani kuti ndiŵayankhe anthu ameneŵa?” Madodawo adamuuza kuti, “Mukaŵachitira chifundo anthu ameneŵa ndi kumaŵasangalatsa, mukalankhula nawo mau abwino, iwowo adzakutumikirani mpaka muyaya.” Koma Rehobowamu adanyozera zimene madoda aja adaamlangiza nakapempha nzeru kwa achinyamata anzake amene adaakula naye pamodzi namamtumikira. Adaŵafunsa kuti, “Kodi mungandilangize zotani kuti tiŵayankhe anthu ameneŵa amene andipempha kuti, ‘Tipeputsireniko goli limene bambo wanu adatisenzetsa?’ ” Achinyamata anzakewo adamuuza kuti, “Anthuwo akupemphani kuti, ‘Bambo wanu adatisenzetsa goli lolemera, koma inu mutipeputsireko.’ Inu tsono mukaŵauze kuti, ‘Chala changa chakaninse nchachikulu kupambana chiwuno cha bambo wanga! Ndiye kuti bambo wanga ankakusenzetsani goli lolemetsa, kuyambira pano ine ndidzaonjezerapo. Bambo wanga ankakukwapulani ndi zikoti wamba, koma ine ndidzakukwapulani ndi mikwapulo yachitsulo.’ ” Tsono Yerobowamu ndi anthu onse adabwera kwa Rehobowamu mkucha wake, monga momwe mfumu idaanenera kuti, “Mubwerenso kuno mkucha.” Ndiye mfumuyo idaŵayankha mwankhanza. Idanyonzera malangizo a madoda aja, nilankhula potsata malangizo a anyamata anzake, nkunena kuti, “Bambo wanga ankakusenzetsani goli lolemetsa, koma ine ndidzaonjezerapo. Bambo wanga ankakukwapulani ndi zikoti wamba, koma ine ndidzakukwapulani ndi mikwapulo yachitsulo.” Choncho mfumuyo sidamvere pempho la anthuwo, pakuti Mulungu anali atazikonzeratu zinthuzo kuti zichitikedi zimene Chauta adaalankhula ndi Yerobowamu, mwana wa Nebati, kudzera mwa Ahiya wa ku Silo. Tsono Aisraele onsewo ataona kuti mfumu sidamvere zimene ankapemphazo, adayankha kuti, “Kodi ife tili ndi gawo lanjinso m'banja la Davide? Sitingayembekeze choloŵa chilichonse m'banja la mwana wa Yese. Ndiye inu Aisraele, bwererani kumahema kwanu. Tsopano iwe mwana wa Davide, udziwonere wekha pa banja lako.” Choncho Aisraele onsewo adachoka napita ku nyumba zao. Koma Rehobowamu adakhala akulamulirabe Aisraele enawo okhala m'mizinda ya ku Yuda. Tsono mfumu Rehobowamu adatuma Adoramu amene ankayang'anira ntchito yathangata, koma anthu a ku Israele adamponya miyala mpaka kumupha. Pamenepo, mfumu Rehobowamu adakwera msangamsanga pa galeta lake nathaŵira ku Yerusalemu. Motero Aisraele akumpoto adakhala akupandukira banja la Davide mpaka lero lino. Rehobowamu atafika ku Yerusalemu, adasonkhanitsa ankhondo osankhidwa okwanira 180,000, afuko la Yuda ndi la Benjamini, ndi cholinga akamenyane nkhondo ndi anthu a ku Israele, kuti choncho ambwezere Rehobowamu ufumu wake. Koma Chauta adadza kwa Semaya, m'meneri wake, namlamula kuti, “Ukauze Rehobowamu, mwana wa Solomoni, mfumu ya ku Yuda, ndi Aisraele onse a ku Yuda ndi a ku Benjamini kuti, ‘Ine Chauta ndikuti, Musapite kukamenyana ndi abale anu. Aliyense abwerere kwao, poti zimene zachitikazi zachokera kwa Ine.’ ” Anthuwo adamvera mau a Chauta, nadabwerera osapita kukamenyana ndi Yerobowamu. Rehobowamu ankakhala ku Yerusalemu, ndipo adamanga mizinda yamalinga ku Yuda. Adamanga Betelehemu, Etamu, Tekowa, Betezuri, Soko, Adulamu, Gati, Maresa, Zifi, Adoraimu, Lakisi, Azeka, Zora, Aiyaloni ndi Hebroni. Mizinda yamalinga yonseyo inali ku Yuda ndi ku Benjamini. Malinga ake adamanga olimba, ndipo adaikamo atsogoleri a nkhondo. Adaikamonso chakudya, mafuta ndi vinyo. Adaikamo zishango ndi mikondo, ndipo adaitchinjiriza kwambiri mizindayo. Choncho ankalamulira anthu a ku Yuda ndi a ku Benjamini. Ansembe pamodzi ndi Alevi amene anali m'dziko lonse la Israele adatsata Rehobowamu, kuchoka konse kumene ankakhala. Alevi adasiya mabusa ao ndi maiko ao, ndipo adapita ku Yuda ndi ku Yerusalemu, chifukwa chakuti Yerobowamu ndi ana ake anali ataŵachotsa pa ntchito zao zaunsembe zomatumikira Chauta. Yerobowamu adaadzisankhira ansembe ake, kuti azitumikira ku kachisi ku zitunda, kupembedza mizimu yoipa ndi mafano a atonde ndi a anaang'ombe amene adaŵapanga. Tsono anthu amene adatsimikiza mumtima mwao kuti azitumikira Chauta, Mulungu wa Israele, ankatsatira ansembe ndi Alevi aja, kuchoka ku mafuko a ku Israele, kupita ku Yerusalemu kukapereka nsembe kwa Chauta, Mulungu wa makolo ao. Iwowo adalimbitsa ufumu wa Yuda, ndipo adamsunga Rehobowamu mwana wa Solomoni zaka zitatu, chifukwa chakuti pa zaka zitatuzo ankatsata chitsanzo cha Davide ndi cha Solomoni. Rehobowamu adakwatira Mahalati, amene bambo wake anali Yerimoti, mwana wa Davide, ndipo mai wake anali Abihaili mwana wa Eliyabu mwana wa Yese. Mkaziyo adambalira ana aŵa: Yeusi, Semariya ndi Zahamu. Adakwatiranso Maaka mwana wa Abisalomu, ndipo adambalira Abiya, Atai, Ziza ndi Selomiti. Rehobowamu ankakonda Maaka mwana wa Abisalomu kupambana akazi ake onse, kupambananso azikazi ake. (Adakwatira akazi 18, ndipo anali ndi azikazi okwanira 60, ndipo anali ndi ana aamuna 28, ana aakazi 60.) Rehobowamu adasankha Abiya, mwana wa Maaka, kuti akhale mtsogoleri pakati pa abale ake, poti ankafuna kuti amlonge ufumu iyeyo. Tsono mwanzeru adaika ena mwa ana ake aamuna m'zigawo zonse za ku Yuda ndi za ku Benjamini, ku mizinda yonse yamalinga. Ankaŵapatsa chakudya chambiri ndi kuŵafunira akazi ochuluka. Rehobowamu atangokhazikitsa ulamuliro wake ndi kuulimbitsa, iyeyo pamodzi ndi Aisraele onse adayamba kusiya malamulo a Chauta. Chaka chachisanu cha ufumu wa Rehobowamu, Sisake mfumu ya ku Ejipito adathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu chifukwa chakuti Aisraele adaakhala osakhulupirika kwa Chauta. Sisakeyo adabwera ndi magaleta ankhondo okwanira 1,200 ndi anthu okwera pa akavalo 60,000. Anthu ake anali osaŵerengeka amene adadza nawo kuchokera ku Ejipito, Libiya, Sukimu ndi Etiopiya. Adalanda mizinda yamalinga ya ku Yuda, nakafika mpaka ku Yerusalemu. Tsono mneneri Semaya adadza kwa Rehobowamu ndi kwa atsogoleri a ku Yuda, amene anali atasonkhana ku Yerusalemu chifukwa cha Sisake, ndipo adaŵauza kuti, “Chauta akunena kuti, ‘Inu mwandisiya Ine, ndiye nanenso ndakusiyani ndi kukuperekani kwa Sisake.’ ” Apo atsogoleri a Aisraele pamodzi ndi mfumu yomwe adadzichepetsa, nati, “Chauta ndi wolungama.” Tsono Chauta ataona kuti anthuwo adzichepetsa, adauzanso Semaya kuti, “Anthuŵa adzichepetsa, sindidzaŵaononga ai, koma ndidzaŵapulumutsa. Sindidzaukwiyira mzinda wa Yerusalemu, motero Sisake sadzauwononga konse. Komabe adzakhala akapolo a Sisakeyo, kuti anthuwo adziŵe kusiyanitsa pakati pa kutumikira Ine ndi kutumikira mafumu a maiko achilendo.” Tsono Sisake, mfumu ya ku Ejipito, adabwera kudzathira Yerusalemu nkhondo. Adalanda chuma cha ku Nyumba ya Chauta pamodzi ndi chuma cha ku nyumba ya mfumu. Adatenga zonse, ngakhalenso zishango zomwe zagolide zimene Solomoni adaapanga. Pambuyo pake mfumu Rehobowamu adapanga zishango zamkuŵa m'malo mwake, nazipereka kwa m'manja mwa akapitao a alonda amene ankalonda pakhomo pa nyumba ya mfumu. Tsono nthaŵi zonse mfumu ikamaloŵa m'Nyumba ya Chauta, alondawo ankatenga zishango, kenaka nkumazibwezera ku chipinda cha alonda. Tsono mfumuyo itadzichepetsa, Chauta adaleka kufuna kuŵaononga kwathunthu. Motero zinthu zinkayenda bwino ku Yuda. Mfumu Rehobowamu adakhazikitsa ufumu wake ku Yerusalemu. Anali wa zaka 41 nthaŵi imene ankayamba kulamulira. Adalamulira zaka 17 ku Yerusalemu, mzinda umene Chauta adausankha pakati pa mafuko onse a Israele kuti azimpembedza kumeneko. Mai wake anali Naama, Mwamoni. Koma Rehobowamuyo adachita zoipa, popeza kuti mtima wake sudafunitsitse Chauta. Tsono ntchito za Rehobowamu kuyambira poyamba mpaka pomaliza, paja zidalembedwa m'buku la mbiri ya mneneri Semaya ndiponso m'buku la mbiri ya mneneri Ido. Panali nkhondo zosakata pakati pa Rehobowamu ndi Yerobowamu. Rehobowamu adamwalira, naikidwa m'manda mu mzinda wa Davide. Tsono Abiya mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Pa chaka cha 18 cha ufumu wa Yerobowamu, Abiya adaloŵa ufumu wa ku Yuda. Adakhala mfumu mu Yerusalemu zaka zitatu. Mai wake anali Maaka, mwana wa Uriyele wa ku Gibea. Tsono panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobowamu. Abiya adanyamuka kupita ku nkhondo atatenga gulu lake la ankhondo olimba mtima okwanira 400,000 osankhidwa. Yerobowamu adandanditsa ankhondo ake oti amenyane ndi Abiya, anthu okwanira 800,000, amphamvu ndi osankhidwa. Tsono Abiya adaima pa phiri la Zemaraimu, limene lili ku dziko lamapiri la Efuremu, ndipo adati, “Iwe Yerobowamu, pamodzi ndi Aisraele onse, imvani zimene ndikunenazi. Kodi simukudziŵa kuti Chauta, Mulungu wa Israele, adapereka ufumu wa Israele kwa Davide ndi kwa ana ake mpaka muyaya, pochita chipangano chosaphwanyika? Komabe Yerobowamu mwana wa Nebati, mtumiki wa Solomoni mwana wa Davide, adanyamuka naukira mbuyakeyo. Ndipo anthu ena achabechabe adasonkhana kwa iye nachita chipongwe Rehobowamu mwana wa Solomoni pa nthaŵi imene Rehonowamu anali wamng'ono ndi wosalimba mtima, ndipo sankatha kulimbana nawo. “Tsopano inu mukuganiza zolimbana ndi ufumu wa Chauta ndi kuulanda m'manja mwa ana a Davide, poti inuyo ndinu ambirimbiri. Ndipo muli nawo mafano agolide, a anaang'ombe amene Yerobowamu adakupangirani, kuti akhale milungu yanu. Kodi inu simudapirikitsa ansembe a Chauta, ana a Aaroni, ndiponso Alevi, ndipo mudadzisankhira ansembe anuanu, monga amachitira anthu a mitundu ina am'maikomo? Munthu aliyense amene amabwera kuti adzipereke atatenga mwanawang'ombe wamphongo kapena nkhosa zamphongo zisanu ndi ziŵiri, amasanduka wansembe wa zinthu zimene sizili milungu konse. Koma kunena za ife, Chauta ndiye Mulungu wathu, ndipo sitidamsiye ai. Tili nawo ansembe, ana a Aaroni, otumikira Chauta, tilinso ndi Alevi amene amatumikira ansembewo. Iwowo amapereka kwa Chauta nsembe zopsereza m'maŵa mulimonse ndi madzulo aliwonse. Amafukiza lubani wonunkhira bwino, amaikanso buledi wopereka pa tebulo la golide weniweni, namasamala zoikapo nyale zagolide, kuti nyale zake ziziyaka madzulo aliwonse. Ife timasunga zimene Chauta Mulungu wathu amatilamula, koma inuyo mudamsiya. Onani, Mulungu ali nafe, akutitsogolera, ansembe ake atatenga malipenga ao ankhondo otiitanira ku nkhondo yokamenyana ndi inu. Inu ana a Israele, musati mulimbane ndi Chauta, Mulungu wa makolo anu, chifukwa simungathe kupambana.” Yerobowamu anali atatumiza anthu obisalira, kuti alimbane nawo moŵadzera kumbuyo. Motero magulu ankhondowo anali kutsogolo kwa anthu a ku Yuda, ndipo obisalirawo anali kumbuyo kwao. Anthu a ku Yuda aja poyang'ana, adangoona kuli nkhondo kutsogolo kwao ndi kumbuyo komwe. Tsono adafuula kwa Chauta, ndipo ansembe adayamba kuliza malipenga. Apo anthu a ku Yuda adafuula, kufuula kwake kwankhondo. Ndipo anthu a ku Yudawo atafuula, Mulungu adagonjetsa Yerobowamu pamodzi ndi anthu a ku Israele onse, pamaso pa Abiya ndi pa anthu a ku Yuda. Aisraele adathaŵa Ayuda, ndipo Mulungu adapereka Aisraelewo kwa Ayuda. Abiya pamodzi ndi anthu ake adapha Aisraelewo, kupha kwake kwakukulu. Adaphedwa Aisraele okwanira 500,000, anthu ndithu osankhidwa. Motero Aisraele adagonjetsedwa nthaŵi imeneyo, ndipo Ayuda adapambana chifukwa chakuti adakhulupirira Chauta, Mulungu wa makolo ao. Tsono Abiya uja adapirikitsa Yerobowamu, namlanda mizinda iyi: Betele ndi midzi yake, Yasana ndi midzi yake, ndiponso Efuroni ndi midzi yake. Yerobowamu sadapezenso mphamvu nthaŵi ya Abiya. Ndipo Chauta adamkantha Yerobowamu, naafa. Koma Abiya mphamvu zake zidakula. Ndipo adakwatira akazi khumi ndi anai, nabala ana aamuna 22 ndi ana aakazi 16. Ntchito zonse za Abiya, makhalidwe ake ndi zimene ankalankhula zidalembedwa m'buku la mbiri ya mneneri Ido. Tsono Abiya adamwalira, naikidwa m'manda mu mzinda wa Davide. Pambuyo pake Asa mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Pa masiku a Asa, dziko lidakhala pa mtendere zaka khumi. Asa adachita zokoma ndi zolungama pamaso pa Chauta, Mulungu wake. Adagwetsa maguwa achilendo, nkuwononga akachisi ku zitunda, nagumula zipilala zamiyala zachipembedzo, nkugwetsa mafano a Asera. Ndipo adalamula anthu a ku Yuda kuti azitembenukira kwa Chauta, Mulungu wa makolo ao, ndi kumamvera malangizo ndi malamulo ake. M'mizinda yonse ya ku Yuda adaononga akachisi opembedzeramo mafano nagumula maguwa ofukizirapo lubani. Ndipo dzikolo lidakhala pa mtendere nthaŵi imene Asa ankalamulira. Adamanga mizinda yamalinga ku Yuda, chifukwa dzikolo linali pa mtendere. Sadamenye nkhondo masiku amenewo, popeza kuti Chauta adampatsa mtendere. Adauza anthu a ku Yuda kuti, “Tiyeni timange mizinda imeneyi, ndipo timange makoma ndi nsanja, zitseko ndi mipiringidzo yake. Dzikoli lidakali lathu, chifukwa chakuti tachita kufuna kwa Chauta, Mulungu wathu. Tachita kufuna kwake, ndipo Iye watipatsa mtendere pa mbali iliyonse.” Choncho adamangadi zimenezo, ndipo adapeza bwino ndithu. Tsono Asa anali nalo gulu lankhondo la anthu 300,000 a ku Yuda. Iwoŵa anali ndi zishango ndi mikondo. Anthu a ku Benjamini analipo 280,000. Iwowo anali ndi zishango ndi mauta. Anthu onsewo anali amphamvu ndi olimba mtima. Zera wa ku Etiopiya adanyamuka kukamenyana ndi Ayuda atatenga gulu lake lankhondo la anthu 1,000,000, ndi magaleta 300, ndipo adakafika mpaka ku Maresa. Tsono Asa adanyamuka kuti akakomane naye, ndipo onsewo adandanditsa magulu ao ankhondo ku chigwa cha Zefati ku Maresa. Pamenepo Asa adafuula kwa Chauta, Mulungu wake, kuti, “Inu Chauta, palibe wina wofanafana nanu woti angathandize pakati pa anthu amphamvu ndi ofooka. Tithandizeni, Inu Chauta, Mulungu wathu, popeza kuti timakhulupirira Inu, ndipo tabwera kudzamenyana ndi chinamtindi cha anthu chimenechi m'dzina lanu. Inu Chauta, ndinu Mulungu wathu. Munthu asakupambaneni ai.” Motero Chauta adagonjetsa anthu a ku Etiopiya pamaso pa Asa ndi pa anthu a ku Yuda, ndipo anthu a ku Etiopiyawo adathaŵa. Asa pamodzi ndi anthu ake aja adaŵathamangitsa mpaka ku Gerari, ndipo anthu a ku Etiopiyawo adaphedwa onse, osatsalapo ndi mmodzi yemwe wamoyo. Zidatero chifukwa anali ndi mantha aakulu pamaso pa Chauta ndi gulu lake lankhondo. Ndipo Ayuda adatenga zofunkha zambirimbiri. Tsono adakantha mizinda yonse yozungulira Gerari pakuti anthu ake adaagwidwa ndi mantha oopa Chauta. Adalanda katundu m'mizinda yonse, poti munali chuma chambiri m'mizindamo. Ndipo adagwetsa makola a ziŵeto, ndi kutenga nkhosa zochuluka, pamodzi ndi ngamira. Kenaka adabwerera ku Yerusalemu. Mzimu wa Mulungu udamtsikira Azariya mwana wa Odedi. Tsono iye adatuluka mu mzinda wake kukakomana ndi Asa, ndipo adamuuza kuti, “Ndimvereni inu Asa, Ayuda nonsenu ndi inu Abenjamini. Chauta ali nanu nthaŵi yonse imene inu muli ndi Iye. Mukamfunafuna mudzampeza. Koma mukamsiya, nayenso adzakusiyani. Pa nthaŵi yaitali Aisraele adakhala opanda Mulungu woona, ndiponso opanda wansembe woŵaphunzitsa, ndipo analibe malamulo. Koma pamene anali pa mavuto, namabwera kudzafunafuna Chauta, Mulungu wa Israele, ankamupeza. Pa masiku amenewo panalibe mtendere kwa munthu amene ankatuluka kapena kuloŵa, pakuti mavuto adaaŵagwera onse amene ankakhala m'makomo. Anthuwo adagalukirana, mtundu wina unkamenyana ndi mtundu wina, mzinda unkamenyana ndi mzinda wina, pakuti Mulungu adaaŵavuta ndi mazunzo osiyanasiyana. Koma inu limbani mtima, manja anu asafooke chifukwa mudzalandira mphotho ya ntchito yanu.” Tsono Asa atamva mau ameneŵa, mau aulosi a Azariya mwana wa Odedi, adalimba mtima. Adachotsa mafano onyansa ku dziko lonse la Yuda ndi la Benjamini. Adachotsanso mafano ku mizinda imene adailanda ku dziko lamapiri la Efuremu. Ndipo adakonza guwa la Chauta limene linali patsogolo pa khonde la Nyumba ya Chauta. Adasonkhanitsa Ayuda onse ndi Abenjamini ndiponso anthu a ku Efuremu, Manase ndi Simeoni amene ankangokhala nao, pakuti anthu ambiri anali atathaŵira kwa mfumu Asa, kuchoka ku Israele, ataona kuti Chauta Mulungu wake anali naye Asayo. Anthuwo adasonkhana ku Yerusalemu pa mwezi wachitatu chaka cha 15 cha ufumu wa Asa. Tsiku limenelo adapereka nsembe kwa Chauta zotapako pa za zofunkha zimene adaabwera nazo, ndiye kuti ng'ombe 700, ndi nkhosa 7,000. Tsono adapangana zoti azifunafuna Chauta, Mulungu wa makolo ao, ndi mtima wao wonse ndi moyo wao wonse. Adaamvana kuti aliyense wosafunafuna Chauta, Mulungu wa Israele, aziphedwa, kaya ndi wamng'ono kaya wamkulu, wamwamuna kapena wamkazi. Zimenezi adalumbira kwa Chauta mokweza mau ndi mofuula, alikuliza malipenga ndi mbetete. Ndipo anthu onse a ku Yuda adakondwa pa mwambo wolumbirirawo, pakuti adalumbira ndi mtima wao wonse. Ankafunafuna Chauta kwambiri, ndipo adampezadi. Motero Chauta adaŵapatsa mtendere ponse poŵazungulira. Mfumu Asa adachotsa ngakhale ufumu wa Maaka, gogo wake, chifukwa choti Maakayo anali atachita chinthu choipa kwambiri popanga fano. Asa adagwetsa fanolo, nalitswanya, ndipo adakalitentha ku mtsinje wa Kidroni. Koma akachisi sadaŵaononge ku Israele. Ngakhale zinali choncho, mtima wa Asa udakhala wangwiro masiku onse a moyo wake. Ndipo adabwera ku Nyumba ya Chauta ndi mphatso zimene bambo wake adaapereka, ndiponso zopereka iye mwini, monga siliva, golide ndi ziŵiya. Tsono panalibenso nkhondo mpaka chaka cha 35 cha ufumu wa Asa. Pa chaka cha 36 cha ufumu wa Asa, Baasa mfumu ya ku Israele, adapita kukathira nkhondo dziko la Yuda. Adamangira linga mzinda wa Rama kuti aziletsa anthu kuloŵa kapena kutuluka m'dziko la Asa, mfumu ya ku Yuda. Tsono Asa adatenga siliva ndi golide ku malo osungira chuma cha ku Nyumba ya Chauta ndiponso ku nyumba ya mfumu, nazitumiza kwa Benihadadi, mfumu ya ku Siriya, amene ankakhala ku Damasiko. Mau a Asa anali akuti, “Tiye tigwirizane ine ndi iwe, monga m'mene ankachitira bambo wanga ndi bambo wako. Ona ndikukutumizira mphatso za siliva ndi golide. Pita ukaphwanye chigwirizano chako ndi Baasa, mfumu ya ku Israele, kuti asadzanditherenso nkhondo.” Benihadadi adamvera zimene adanena mfumu Asa zija, motero adatuma atsogoleri a magulu ake ankhondo kukathira nkhondo mizinda ya ku Israele. Adagonjetsa Iyoni, Dani, Abele-Maimu ndi mizinda yonse ya ku Nafutali yosungiramo zinthu. Tsono Baasa atazimva zimenezi, adaleka kumangira Rama linga ndipo ntchito yonseyo adaisiya. Apo mfumu Asa adabwera ndi Ayuda onse, ndipo adadzanyamula miyala ndi mitengo imene Baasa ankamangira linga la Rama. Zimenezi Asa adamangira linga la Geba ndi la Mizipa. Nthaŵi imeneyo mneneri Hanani adadza kwa Asa mfumu ya ku Yuda, namuuza kuti, “Chifukwa chakuti mudakhulupirira mfumu ya ku Siriya, osakhulupirira Chauta, Mulungu wanu, gulu lankhondo la mfumu ya ku Siriya lakuthaŵirani. Kodi Aetiopiya ndi Alibiya sanali gulu lalikulu lankhondo, lokhala ndi magaleta ochuluka ndiponso anthu ambirimbiri okwera pa akavalo? Komabe chifukwa chodalira Chauta, Chautayo adaŵapereka kwa inu. Paja maso a Chauta amayang'ana uku ndi uku pa dziko lonse lapansi, kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wao uli wangwiro kwa Iyeyo. Inuyo mwachita zopusa pa zimenezi. Ndiye kuyambira tsopano lino, mpaka m'tsogolo muno, mudzakhala pa nkhondo.” Apo Asa adapsera mtima mneneriyo, ndipo adammanga namuika m'ndende, popeza kuti adaakwiya naye kwambiri chifukwa cha zimenezi. Kenaka Asayo adayamba kuchita zankhalwe pa anthu enanso nthaŵi yomweyo. Tsono ntchito za Asa, kuyambira pa chiyambi mpaka pomaliza, zidalembedwa m'buku la Mafumu a ku Yuda ndi a ku Israele. Pa chaka cha 39 cha ufumu wake, Asa adayamba kudwala nthenda ya mapazi, ndipo nthendayo idakula kwambiri. Komabe ngakhale ankadwala choncho, sadapemphe chithandizo kwa Chauta, koma kwa asing'anga. Tsono adamwalira, pa chaka cha 41 cha ufumu wake. Adamuika m'manda amene iyeyo adaadzisemera mu mzinda wa Davide. Adagoneka mtembo wake pa chithatha chimene adaikapo zonunkhira zamitundumitundu zimene anthu opanga zonunkhira adazikonza. Ndipo adasonkha chimoto chachikulu kwambiri chomchitira ulemu. Yehosafati, mwana wa Asa, adaloŵa ufumu m'malo mwa bambo wake, ndipo adadzilimbitsa pofuna kulimbana ndi Aisraele. Adaika magulu ankhondo ku mizinda yonse yamalinga ya ku Yuda, ndipo adamanga maboma ankhondo ku dziko la Yuda ndi ku mizinda ya ku Efuremu, imene Asa bambo wake adailanda. Chauta anali naye Yehosafati, chifukwa chakuti ankatsata makhalidwe oyambayamba aja a Asa bambo wake. Sadatsate Abaala, koma ankatsata Mulungu wa atate ake, ndipo ankasunga malamulo ake, osatsata makhalidwe a Aisraele. Nchifukwa chake Chauta adaukhazikitsa ufumuwo m'manja mwake. Anthu onse a ku Yuda ankakhoma msonkho kwa iyeyo. Choncho anali nacho chuma chambiri ndiponso ulemu. Iyeyo adalimba mtima pa zinthu za Chauta. Kuwonjezera pamenepo, adathetsa akachisi ndiponso mafano a Aserimu ku Yuda. Pa chaka chachitatu cha ufumu wake, Yehosafati adatuma nduna zake, Benihali, Obadiya, Zekariya, Netanele ndi Mikaya, kuti akaphunzitse ku mizinda ya ku Yuda. Adapita ndi Alevi aŵa: Semaya, Netaniya, Zebadiya, Asahele, Semiramoti, Yohonatani, Adoniya, Tobiya ndi Tobadoniya. Alevi ameneŵa anali pamodzi ndi ansembe aŵa: Elisama ndi Yehoramu. Ankaphunzitsa ku Yuda, ali ndi buku la malamulo a Chauta. Ndipo adayendera mizinda yonse ya ku Yuda, namaphunzitsa pakati pa anthu. Maufumu onse a m'maiko ozungulira Yuda ankaopa Chauta, ndipo sadachitenso nkhondo ndi Yehosafati. Afilisti ena adabwera ndi mphatso kwa Yehosafatiyo, pamodzi ndi siliva wa msonkho. Arabu nawonso adabwera ndi nkhosa zamphongo 7,700 ndi atonde 7,700. Ndipo mphamvu za Yehosafati zidanka zikulirakulira. Ku Yuda adamanga malinga ndi mizinda yosungirako zinthu. Choncho anali ndi nyumba zikuluzikulu zosungiramo zinthu ku mizinda ya ku Yuda. Ku Yerusalemu anali ndi ankhondo, anthu amphamvu ndi olimba mtima. Chiŵerengero chao potsata mabanja ao chinali chotere: Ku Yuda, atsogoleri a zikwi anali aŵa: Adina amene anali ndi anthu amphamvu ndi olimba mtima 300,000. Yehohanani, mtsogoleri wotsatana ndi iyeyo, anali ndi anthu 280,000. Amasiya mwana wa Zikiri, mtsogoleri wotsatana naye, amene adaadzipereka mwaufulu ku ntchito ya Chauta, anali ndi anthu amphamvu ndi olimba mtima 200,000. (Amasiya adadzipereka kutumikira Ambuye.) Ku Benjamini, Eliyada munthu wolimba mtima, anali ndi anthu 200,000 amauta ndi azishango. Yehozabadi anali mtsogoleri wotsatana ndi iyeyo, ndipo anali ndi anthu okonzekera nkhondo 180,000. Ameneŵa ndiwo ankatumikira mfumu, pamodzi ndi ena amene mfumu idaŵaika ku mizinda yamalinga ku dziko lonse la Yuda. Yehosafati anali ndi chuma chambiri ndi ulemerero waukulu. Tsono adachita chigwirizano chaukwati ndi banja la Ahabu. Patapita zaka zina, Yehosafatiyo adapita kwa Ahabu ku Samariya. Ahabuyo adapha nkhosa ndi ng'ombe zambirimbiri kuphera Yehosafatiyo ndi anthu amene anali naye, pofuna kumkopa kuti akalimbane ndi Ramoti-Giliyadi. Ndiye Ahabu mfumu ya ku Israele adafunsa Yehosafati mfumu ya ku Yuda kuti, “Kodi udzapita nane limodzi ku Ramoti-Giliyadi?” Iyeyo adayankha kuti, “Ine ndili nanu limodzi, anthu anga nganu. Ifeyo tidzakhala nanu pa nkhondo.” Yehosafati adauza mfumu ya ku Israele kuti, “Poyamba upemphe nzeru kwa Chauta.” Tsono mfumu ya ku Israele idasonkhanitsa aneneri ake 400, ndipo idaŵafunsa kuti, “Kodi ife tipite kukamenyana nkhondo ndi Ramoti-Giliyadi, kaya kapena ineyo ndileke?” Aneneriwo adamuuza kuti, “Pitani, pakuti Mulungu aupereka mzindawo kwa inu mfumu.” Koma Yehosafati adafunsa kuti, “Kodi pano palibe mneneri wina wa Chauta woti tipempheko nzeru?” Mfumu ya ku Israele idauza Yehosafati kuti, “Alipo wina amene angapemphe nzeru kwa Chauta, dzina lake ndi Mikaya mwana wa Imila. Koma ine ndimadana naye ameneyo popeza kuti sandilosera zabwino, nthaŵi zonse amangondilosera zoipa.” Tsono Yehosafati adati, “Iyai mfumu, musatero.” Apo mfumu ya ku Israele idaitana imodzi mwa nduna nkuiwuza kuti, “Takaitanani Mikaya, mwana wa Imila, abwere kuno msanga.” Nthaŵi imeneyo mfumu ya ku Israele ndi Yehosafati mfumu ya ku Yuda adaakhala pa mipando yao yaufumu, atavala zovala zao zaufumu. Pamenepo panali pa bwalo lopererapo tirigu, pa khomo la chipata cha Samariya. Ndipo aneneri onse ankalosa pamaso pa mafumuwo. Wina mwa iwo, Zedeki, mwana wa Kenana, adaadzisulira nyanga zachitsulo. Iyeyo adati, “Chauta akunena kuti, ‘Ndi nyangazi udzamegonjetsa Asiriya ndi kuŵaonongeratu.’ ” Aneneri onsewo adalosa chimodzimodzi, adati, “Pitani ku Ramoti-Giliyadi, ndipo mukapambana. Chauta aupereka mzindawo kwa inu mfumu.” Wamthenga uja amene adaapita kukaitana Mikaya, adamuuza Mikayayo kuti, “Onani, mau onse amene akunena aneneri, akulosera mfumu zabwino. Ndiye nanunso mau anu akhale ofanafana ndi mau awo. Muzilosa zabwino.” Koma Mikaya adati, “Pali Chauta wamoyo, zimene Mulungu wanga andiuze, ndizo ndidzalankhule.” Tsono atafika kwa Ahabu, mfumuyo idamufunsa kuti, “Kodi Mikaya, ife tipite kukamenya nkhondo ku Ramoti-Giliyadi, kapena ineyo ndileke?” Iye adayankha kuti, “Pitani, mukapambana, anthuwo akaperekedwa kwa inu.” Koma mfumuyo idamufunsa kuti, “Kodi ndikulumbiritse kangati, kuti undiwuze zoona zokhazokha m'dzina la Chauta?” Mikaya adati, “Ndidaona Aisraele onse atamwazikana pa mapiri ngati nkhosa zopanda mbusa. Tsono Chauta adati, ‘Ameneŵa alibe mbuyawo. Aliyense apite kwao mwamtendere.’ ” Pamenepo mfumu ya ku Israele adauza Yehosafati kuti, “Suja ndidaakuuzani kuti ameneyu sadzandilosera zabwino koma zoipa zokha?” Apo Mikaya adati, “Mverani tsono mau a Chauta. Ine ndidapenya Chauta atakhala pa mpando wake waufumu, gulu lonse lakumwamba litaima ku dzanja lake lamanja ndi ku dzanja lake lamanzere. Tsono Chauta adati, ‘Kodi ndani amene akamnyengerere Ahabu mfumu ya ku Israele, kuti akafe ku Ramoti-Giliyadi?’ Wina ankanena zina, winanso nkumanena zina. Apo mzimu wina udadzaima pamaso pa Chauta, nunena kuti, ‘Ndikamnyengerera ndine.’ Tsono Chauta adaufunsa kuti, ‘Ukamnyengerera bwanji?’ Udati, ‘Ndidzapita, nkumakanena zabodza kudzera mwa aneneri ake onse.’ Pamenepo Chauta adati, ‘Ukakatero, ukakhozadi. Pita ukamnyengerere.’ Tsonotu ngati Chauta waika mzimu wabodza m'kamwa mwa aneneri anuŵa, ndiye kuti Iye yemwe waneneratu kuti mukaona tsoka.” Tsono Zedeki uja, mwana wa Kenana, adadza pafupi namenya Mikaya pa tsaya, namufunsa kuti, “Kodi mzimu wa Chauta udadzera njira iti kuti uchoke mwa ine, uzikalankhula ndi iwe?” Mikaya adati, “Udzadziŵa pa tsiku limene uzikaloŵa m'chipinda china ndi china cham'kati kuti ukabisale.” Pamenepo Ahabu, mfumu ya ku Israele, adati, “Mgwireni Mikayayu, mupite naye kwa Amoni, mkulu wa mzinda, ndiponso kwa Yowasi mwana wa mfumu. Mukaŵauze mau angaŵa akuti, ‘Munthu uyu muikeni m'ndende, ndipo muzimpatsa chakudya pang'ono ndi madzi pang'ono, mpaka ine nditabwerera mwamtendere.’ ” Mikaya adati, “Mukabwerera mwamtendere, ndiye kuti Chauta sadalankhule kudzera mwa ine.” Ndipo adaonjeza kuti, “Anthu nonsenu, mumve zimene ndanenazi.” Zitatero Ahabu, mfumu ya ku Israele, ndi Yehosafati mfumu ya ku Yuda, adapita ku Ramoti-Giliyadi. Mfumu ya ku Israele idauza Yehosafati kuti, “Ine ndidzizimbayitsa, ndipo ndipita kunkhondoko, koma iwe uvale malaya ako aufumu.” Choncho mfumu ya ku Israele idadzizimbayitsa, onsewo nkupita ku nkhondo. Mfumu ya ku Siriya nkuti italamula oyendetsa magaleta kuti asamenye nkhondo ndi wina aliyense, wamng'ono kapena wamkulu, koma mfumu ya ku Israele basi. Tsono pamene oyendetsa magaletawo adaona Yehosafati, adati, “Ndithudi ameneyo ndiye mfumu ya ku Israele.” Choncho adabwerera kudzalimbana naye. Koma Yehosafati adayamba kufuula, ndipo Chauta adamthandiza. Mulungu adaŵabweza m'mbuyo. Ndiye kuti oyendetsa magaleta aja ataona kuti ameneyu si mfumu ya ku Israele, adabwerera osamtsatanso. Koma munthu wina adakoka uta wake mwachiponyeponye, ndipo adalasa mfumu ya ku Israele pa maluma a malaya ake achitsulo. Pamenepo mfumuyo idauza woyendetsa galeta lake kuti, “Bwerera, undichotse pankhondo pano chifukwa ndavulazidwa.” Nkhondo idakula kwambiri tsiku limenelo, mwakuti mfumu ya ku Israeleyo idangokhala tsonga m'galeta lake itayang'anana ndi Asiriya mpaka madzulo. Motero pamene dzuŵa linkaloŵa, idafa. Yehosafati mfumu ya ku Yuda adabwerera kunyumba kwake ku Yerusalemu mwamtendere. Koma mneneri Yehu, mwana wa Hanani, adatuluka kuti akumane naye, ndipo adafunsa mfumu Yehosafati kuti, “Kodi ndi bwino kuŵathandiza anthu oipa amene amadana ndi Chauta? Chifukwa cha zimenezi mkwiyo wa Chauta ulikudza kwa inu. Komabe pali zina zabwino zimene mudachita, pakuti mudaononga mafano a m'dziko muno, ndipo mwakhala mukulimbikira ndi mtima wonse kufunafuna Mulungu.” Yehosafati ankakhala ku Yerusalemu. Adayendera anthu kuchokera ku Beereseba mpaka ku dziko lamapiri la ku Efuremu, naŵabweza kwa Chauta, Mulungu wa makolo ao. Adaika anthu oweruza m'dzikomo, mu mzinda uliwonse wamalinga wa ku Yuda. Tsono adauza aweruziwo kuti, “Muganize bwino zimene mukuchita, pakuti simukuweruza m'dzina la munthu ai, koma m'dzina la Chauta. Chautayo ali nanu pamene mukuweruza. Tsono khalani anthu oopa Chauta. Muzisamala zimene mukuchita, pakuti Chauta, Mulungu wathu, sapotoza chiweruzo, kapena kukondera, kapenanso kulandira ziphuphu.” Ku Yerusalemuko Yehosafati adaika Alevi ena ndi ansembe ndiponso akulu a mabanja a Aisraele, kuti aziweruza m'dzina la Chauta ndi kugamula milandu ya anthu. Iwoŵa ankakhala ku Yerusalemu. Adaŵalamula kuti, “Muzichita ntchito imeneyi moopa Chauta, mokhulupirika, ndiponso ndi mtima wonse. Pakakhala mlandu wokhudza abale anu amene akukhala m'mizinda yao, monga mlandu wokhetsa magazi, kapena mlandu wa kusamvera malamulo kapena malangizo kapena zogamula zina, muziŵaphunzitsa nthaŵi zonse kuti asamachimwe pamaso pa Chauta. Motero mkwiyo wa Chauta sudzakugwerani inuyo ndi abale anu. Muzichita choncho, ndipo simudzachimwa konse. Tsono Amariya, mkulu wa ansembe, ndiye adzakhale wokutsogolerani pa zonse zokhudza Chauta. Zebadiya mwana wa Ismaele, kazembe wa fuko la Yuda, ndiye aziyang'anira zonse zokhudza mfumu. Ndipo Alevi adzakutumikirani ngati akapitao. Muzichita zimenezi molimba mtima, Chauta akhale naye amene ali wolungama.” Nthaŵi ina, Amowabu, Aamoni ndi Ameuni ena adabwera kudzamenyana nkhondo ndi Yehosafati. Anthu ena adadzauza Yehosafati kuti “Chinamtindi cha anthu chikudzamenyana nanu nkhondo, kuchokera ku Edomu patsidya pa nyanja. Anthuwo ali ku Hazazoni-Tamara,” (ndiye kuti Engedi). Pamenepo Yehosafati adachita mantha, ndipo adaganiza zopempha nzeru kwa Chauta, nalengeza kuti anthu onse a ku dziko la Yuda asale zakudya. Ayuda onse adasonkhana kuti adzapemphe chithandizo kwa Chauta. Anthu onse a ku mizinda yonse ya ku Yuda adabwera kudzapempha chithandizo kwa Chauta. Tsono Yehosafati adaimirira pakati pa msonkhano wa Ayuda ku Yerusalemu m'Nyumba ya Chauta pa bwalo latsopano. Ndipo adati, “Chauta, Mulungu wa makolo athu, kodi Inu sindinu Mulungu Wakumwamba? Kodi suja mumalamulira maufumu onse a mitundu ya anthu? M'manja mwanu muli mphamvu ndi nyonga, kotero kuti palibe ndi mmodzi yemwe woti nkulimbana nanu. Kodi Inu, Mulungu wathu, suja mudapirikitsa nzika za dziko lino pamene ankafika Aisraele, anthu anu, ndi kulipereka kwa zidzukulu za Abrahamu, bwenzi lanu mpaka muyaya? Mwakuti iwo atakhazikika m'dziko limenelo, adakumangirani Nyumba m'menemo, nkumati, ‘Choipa chikatigwera mwachilango, monga nkhondo, mlili kapena njala, tidzaima m'Nyumba ino ndiponso pamaso panu, popeza kuti dzina lanu lili m'Nyumba muno. Tsono tidzalira kwa Inu pa mavuto athu, Inuyo mudzamva, ndipo mudzatipulumutsa.’ Pajatu pamene Aisraele ankachoka ku Ejipito, simudalole kuti aŵathire nkhondo Aamoni, Amowabu ndi anthu a ku phiri la Seiri. Onsewo adaŵaleka osaŵaononga. Koma tsopano chimene akutibwezera nkudzatipirikitsa m'dziko limene Inu mudatipatsa kuti likhale choloŵa chathu. Inu Mulungu wathu, monga simuŵalanga iwoŵa? Ife tilibe mphamvu zoti nkulimbana nacho chinamtindi chikudzatithira nkhondocho. Tikusoŵa chochita, maso athu ali pa Inu.” Nthaŵi imeneyo nkuti anthu onse a dziko la Yuda ataimirira pamaso pa Chauta, pamodzi ndi akazi ao ndi ana ao ndi ang'onoang'ono omwe. Ndipo mumsonkhanomo mzimu wa Chauta udatsikira Yehaziele, mwana wa Zekariya, mwana wa Benaya, mwana wa Yeiyele, mwana wa Mataniya, mlevi, mmodzi mwa ana a Asafu. Iyeyo adati, “Mverani Ayuda nonsenu, ndi inu nonse okhala ku Yerusalemu, ndi inunso mfumu Yehosafati. Chauta akukuuzani kuti, ‘Musaope, ndipo musataye nacho mtima chinamtindi cha anthuchi, pakuti nkhondo si yanu, nja Mulungu. Maŵa mupite mukamenyane nawo nkhondo. Adzabwera ndipo adzadzera cha ku chikwera cha Zizi. Mudzaŵapeza pafupi ndi chigwa cha kuvuma kwa chipululu cha Yeruwele. Sikudzafunika kuti mumenyane nawo pa nkhondo imeneyi. Inu mukhale m'malo mwanu, mungoima, ndipo muwonerere Chauta akukumenyerani nkhondo, inu anthu a ku Yuda ndi inu anthu a mu Yerusalemu.’ Musaope ndipo musataye mtima, mutuluke maŵa mukalimbane nawo, Chauta adzakhala nanu.” Apo Yehosafati adazyolikitsa nkhope yake pansi, ndipo anthu onse a ku Yuda ndi anthu onse a ku Yerusalemu adagwa pansi pamaso pa Chauta nampembedza. Kenaka Alevi, ana a Kohati ndi ana a Kora, adaimirira kuti atamande Chauta, Mulungu wa Aisraele, mokweza kwambiri. Tsono anthuwo adadzuka m'mamaŵa nakaloŵa m'chipululu cha ku Tekowa. Pamene ankatuluka, Yehosafati adaima nati, “Tamverani inu anthu a ku Yuda ndi inu okhala mu Yerusalemu. Khulupirirani Chauta, Mulungu wanu, ndipo mudzalimbika, khulupirirani aneneri ake, ndipo mudzapambana.” Tsono ataŵafunsa anthuwo, adasankha ena oti aziimbira Chauta ndi kumtamanda, oimbawo atavala zovala zoyera, akutsogolera gulu lankhondo namanena kuti, “Thokozani Chauta, pakuti chikondi chake chosasinthika chimakhala mpaka muyaya.” Iwo aja atayamba kuimba ndi kutamanda, Chauta adaŵatchera msampha Aamoni, Amowabu ndiponso anthu a ku phiri la Seiri, amene adaadzalimbana ndi anthu a ku Yuda, kotero kuti adaŵagonjetsa onse. Aamoni ndi Amowabu adaukira anthu okhala ku phiri la Seiri, naŵaononga kotheratu. Ndipo ataononga anthu onse a ku Seiri aja, adayamba kumaphana okhaokha. Pambuyo pake anthu a ku Yuda atafika ku nsanja yakuchipululu, adapenya kumene kunali chinamtindi cha anthu chija. Adangoona mitembo yokhayokha ili pansi ngundangunda. Panalibe ndi mmodzi yemwe wopulumuka. Tsono Yehosafati ndi anthu ake atadzafunkha za anthuwo, adapeza ng'ombe zambirimbiri, katundu, zovala ndiponso zinthu zamtengowapatali. Adatenga zinthu zochuluka, mpaka kuzilephera. Adafunkha zinthuzo masiku atatu, chifukwa zinali zambirimbiri. Pa tsiku lachinai lake, adasonkhana ku chigwa cha Beraka, ndipo kumeneko adatamanda Chauta. Nchifukwa chake malowo amatchedwa chigwa cha Beraka mpaka lero lino. Tsono onsewo a ku Yuda ndi a mu Yerusalemu adabwerera mokondwa ku Yerusalemu, Yehosafati akuŵatsogolera, pakuti Chauta adaŵakondweretsa poŵagonjetsera adani ao. Anthuwo adafika ku Yerusalemu, ku Nyumba ya Chauta, akuimba azeze, apangwe ndiponso malipenga. Ndipo maufumu onse a m'maiko achilendowo adachita mantha kwambiri, atamva kuti Chauta ndiye adathira nkhondo pa adani a Aisraele. Motero mudakhala bata mu ufumu wonse wa Yehosafati, pakuti Mulungu adampatsa mtendere ku maiko onse omzungulira. Choncho Yehosafati adayamba kulamulira Yuda. Anali wa zaka 35 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 25 ku Yerusalemu. Mai wake anali Azuba, mwana wa Sili. Yehosafati ankayenda motsata chitsanzo chabwino cha Asa atate ake. Sadapatuke pa zimenezo. Ankachita zolungama pamaso pa Chauta. Komabe akachisi opembedzerako mafano sadaŵaononge. Anthu anali asanapereke mitima yao kwa Mulungu wa makolo ao. Tsono ntchito zonse zimene adachita Yehosafati kuyambira poyamba mpaka potsiriza, zidalembedwa m'buku la mbiri ya Yehu, mwana wa Hanani, limene lili chigawo cha buku lokamba za mafumu a Aisraele. Zitapita zimenezi, Yehosafati mfumu ya ku Yuda, adagwirizana ndi Ahaziya mfumu ya ku Israele, amene ankachita zoipa kwambiri. Adagwirizana naye pomanga zombo zomapita ku Tarisisi ndipo zombozo ankazimangira ku Eziyoni-Gebere. Tsono Eliyezere mwana wa Dodavahu wa ku Maresa, adalosa zoipira Yehosafati adati, “Chifukwa chakuti mwagwirizana ndi Ahaziya, Chauta adzaononga zimene mwapangazo.” Ndipo zombozo zidaonongekadi zosakafika ku Tarisisi. Yehosafati adamwalira, naikidwa m'manda momwe adaaikidwa makolo akewo mu mzinda wa Davide. Tsono Yehoramu mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Abale ake, ana a Yehosafati, anali aŵa: Azariya, Yehiyele, Zekariya, Azariyahu, Mikaele ndi Sefatiya. Onseŵa anali ana a Yehosafati, mfumu ya ku Yuda. Atate ao adaaŵapatsa mphatso zambiri za siliva, golide, ndi zinthu zamtengowapatali, pamodzi ndi mizinda yamalinga ya ku Yuda. Koma ufumu adapatsa Yehoramu, chifukwa chakuti anali mwana wachisamba. Yehoramu ataloŵa ufumu, nakhazikika pa mpando waufumu wa atate akewo, adapha abale ake onse ndi lupanga, ngakhalenso atsogoleri ena a ku Israele. Yehoramu anali wa zaka 32 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka zisanu ndi zitatu ku Yerusalemu. Ankatsata makhalidwe a mafumu a ku Israele, monga m'mene linkachitira banja la Ahabu, pakuti adaakwatira mwana wa Ahabu. Tsono ankachita zoipa zilizonse pamaso pa Chauta. Komabe Chauta sadafune kuononga banja la Davide, chifukwa cha chipangano chimene adaachita ndi Davide, ndiponso poti adaalonjeza kuti adzampatsa nyale Davide ndi zidzukulu zake mpaka muyaya. Pa nthaŵi yakeyo anthu a ku Edomu adaukira ulamuliro wa Yuda, ndipo adadzisankhira mfumu yao. Tsono Yehoramu adapita pamodzi ndi atsogoleri ake ankhondo ndi magaleta ake onse. Adanyamuka usiku nakaŵakantha Aedomu amene adaamzinga iyeyo pamodzi ndi atsogoleri a magaleta ake. Choncho Aedomu ngoukira ulamuliro wa Yuda mpaka lero lino. Pa nthaŵi imeneyo, mzinda wa Libina nawonso udaukira ulamuliro wa Yehoramuyo, chifukwa chakuti adaasiya Chauta, Mulungu wa makolo ake. Kubzolera pamenepo adayambitsa akachisi opembedzerako mafano ku dziko lamapiri la ku Yuda, ndipo adatsogolera anthu a ku Yerusalemu kuti akhale osakhulupirika, nasokeza anthu a ku Yuda. Tsono adalandira kalata kwa mneneri Eliya, yonena kuti, “Chauta, Mulungu wa Davide, kholo lanu, akunena kuti, ‘Sudatsate chitsanzo cha Yehosafati bambo wako, kapenanso cha Asa, mfumu ya ku Yuda, koma watsata chitsanzo cha mafumu aku Israele. Watsogolera anthu a ku Yuda pamodzi ndi anthu a mu Yerusalemu kuti akhale osakhulupirika, monga m'mene linkachitira banja la Ahabu pochimwitsa anthu a ku Israele. Wapha abale ako a pa banja la atate ako, amene anali abwino kupambana iwe. Chifukwa cha zonsezi Chauta adzaŵagwetsera mliri anthu ako, ana ako, akazi ako, ndi zinthu zako zonse. Ndipo iweyo udzadwala nthenda yoopsa ya m'mimba imene izidzakulirakulira tsiku ndi tsiku mpaka matumbo ako adzasololoka.’ ” Tsono Chauta adamuutsira Yehoramuyo mkwiyo wa Afilisti ndi mkwiyo wa Arabu amene ali pafupi ndi Aetiopiya. Motero iwowo adadzalimbana ndi anthu a ku Yuda naŵathira nkhondo. Ndipo adalanda zinthu zonse zimene adazipeza ku nyumba ya mfumu, pamodzinso ndi ana ake aamuna ndi akazi ake, kotero kuti panalibe mwana ndi mmodzi yemwe wamwamuna amene adatsala, kupatula Ahaziya mzime wake. Pambuyo pake Chauta adamkantha ndi nthenda ya m'mimba yosachizika. Patapita nthaŵi ndithu, pomatha chaka chachiŵiri, matumbo ake adayamba kusololoka chifukwa cha nthendayo, ndipo adafa imfa yopweteka kwambiri. Anthu sadasonkhe moto kuti amchitire ulemu monga m'mene ankachitira ndi makolo ake. Iyeyo anali wa zaka 32 pamene ankayamba ufumu wake, ndipo adalamulira zaka zisanu ndi zitatu ku Yerusalemu. Adafa popanda munthu womumvera chisoni. Adamuika mu mzinda wa Davide, koma osati m'manda a mafumu. Anthu okhala mu Yerusalemu adalonga ufumu Ahaziya, mzime wa Yehoramu uja, m'malo mwa bambo wakeyo, pakuti gulu lankhondo limene lidadza pamodzi ndi Arabu kuzithandoko, linali litapha ana onse akuluakulu aamuna. Motero Ahaziya, mwana wa Yehoramu mfumu ya ku Yuda, ndiye amene adaloŵa ufumu. Ahaziyayo anali wa zaka 42 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira chaka chimodzi ku Yerusalemu. Mai wake anali Ataliya, mdzukulu wake wa Omuri. Iyeyonso ankatsata chitsanzo cha banja la Ahabu, poti mai wake ndiye ankamupatsa uphungu woipa. Adachita zoipa pamaso pa Chauta, monga momwe linkachitira banja la Ahabu. Pakuti atafa bambo wake uja, anthuwo ndiwo amene ankamupatsa uphungu pa ntchito zake zoipa. Iyeyo adatsatanso uphungu wao, ndipo adapita pamodzi ndi Yoramu, mwana wa Ahabu mfumu ya ku Israele, kuti akamenyane nkhondo ndi Hazaele, mfumu ya ku Siriya, ku Ramoti ku Giliyadi. Kumeneko Asiriya adamlasa Yoramu. Tsono iye adabwerera napita ku Yezireele kuti akamchiritse mabala amene adaamlasa ku Rama, pamene ankamenyana ndi Hazaele mfumu ya ku Siriya. Motero Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya ku Yuda adapita ku Yezireele kukazonda Yoramu, mwana wa Ahabu, chifukwa chakuti ankadwala. Koma Mulungu adazikonzeratu kuti Ahaziya aonongedwe pokacheza kwa Yoramuyo. Atafika kumeneko, adapita pamodzi ndi Yoramu kuti akakumane ndi Yehu, mwana wa Nimisi, amene Chauta adaamsankha kuti aononge banja la Ahabu. Pamene Yehu ankalanga banja la Ahabu lija, adakumana ndi atsogoleri a ku Yuda ndiponso ana aamuna a abale ake a Ahaziya, amene ankatumikira Ahaziya, iye nkuŵapha onsewo. Adafunafuna Ahaziya, ndipo adamgwira pamene ankabisala ku Samariya. Adabwera naye kwa Yehu, namupha. Anthuwo adamuika m'manda, poti ankati, “Ameneyu ndi mdzukulu wa Yehosafati uja amene ankatumikira Chauta ndi mtima wake wonse.” Choncho banja la Ahaziya linalibe munthu woti nkukhala mfumu yomalamulira. Tsono Ataliya, mai wake wa Ahaziya, ataona kuti mwana wake wafa, adanyamuka nakaononga onse a pa banja laufumu la Yuda. Koma Yehoseba, mwana wamkazi wa mfumu, adatenga Yowasi mwana wa Ahaziya. Adachita momuba, kumuchotsa pakati pa ana aamuna a mfumu amene ankati aŵaphewo. Adamuika m'chipinda china chogona cha m'Nyumba ya Chauta pamodzi ndi mlezi wake. Motero Yehoseba, mwana wamkazi wa mfumu Yehoramu, mkazi wake wa wansembe Yehoyada, poti anali mlongo wake wa Ahaziya, adambisa mwanayo, kotero kuti Ataliya sadamuphe. Mwanayo adakhala ndi iwowo zaka zisanu ndi chimodzi, akubisala m'Nyumba ya Chauta, pamene Ataliya ankalamulira dzikolo. Koma pa chaka chachisanu ndi chiŵiri, wansembe Yehoyada adalimba mtima, naitana anthu aŵa, amene anali atsogoleri a anthu mazana: Azariya, mwana wa Yerohamu, Ismaele mwana wa Yehohanani, Azariya mwana wa Obedi, Maaseiya mwana wa Adaya ndi Elisafati mwana wa Zikiri. Iwoŵa adayendera dziko la Yuda, nasonkhanitsa Alevi onse a ku mizinda yonse ya ku Yuda ndi atsogoleri a mabanja a Aisraele, nabwera onse ku Yerusalemu. Msonkhano wonsewo udachita chipangano ndi mfumu m'Nyumba ya Mulungu. Yehoyada adaŵauza anthuwo kuti, “Nayu mwana wa mfumu. Iyeyu akhale mfumu monga Chauta adanenera za ana a Davide. Zimene mudzachite ndi izi: mwa inu ansembe ndi Alevi amene mukudzatumikira pa sabata, mugaŵikane patatu: gulu limodzi lidzalonde pa makomo. Gulu lachiŵiri lidzalonde ku nyumba ya mfumu, gulu lachitatu lidzalonde pa khomo lakuchipata. Ndipo anthu onse adzakhale m'mabwalo a Nyumba ya Chauta. Musalole aliyense kuti aloŵe m'Nyumba ya Chauta, koma ansembe ndi Alevi okha amene amatumikira. Iwo angathe kuloŵa poti ngoyeretsedwa. Anthu onse azimvera lamulo la Chauta. Alevi akhale moizungulira mfumu, aliyense atatenga zida m'manja. Wina aliyense amene ati aloŵe m'Nyumbamo aphedwe. Muzikhala nayo mfumu kulikonse kumene iziyenda.” Alevi ndi anthu onse a ku Yuda adachitadi zonse monga m'mene wansembe Yehoyada adaŵalamulira. Aliyense adabwera ndi anthu ake amene ankadzayamba ntchito yao yotumikira pa sabata, pamodzinso ndi anthu amene ankasiya ntchito yao yotumikira pa sabata. Pakuti wansembe Yehoyada sadaŵaloleze kuchokapo. Tsono Yehoyadayo adapatsa atsogoleri aja mikondo ndi zishango zazikulu ndi zazing'ono, zimene zidaali za mfumu Davide. Zimenezi zinkasungidwa mu Nyumba ya Chauta. Adandanditsa anthu onsewo kuti aziteteza mfumu, aliyense ali ndi mkondo m'manja, kuyambira kumwera kwa Nyumbayo mpaka kumpoto kwake, pafupi ndi guwa mpaka pa khomo la Nyumba kuti azizungulira mfumu. Kenaka adaŵatulutsira mwana wa mfumu, namuveka chisoti chaufumu, nkumupatsa buku la malamulo, ndipo adamlonga ufumu. Tsono Yehoyada pamodzi ndi ana ake adamdzoza, anthu nafuula kuti, “Amfumu akhale ndi moyo wautali.” Tsono Ataliya atamva phokoso la anthu othamangira komweko akutamanda mfumu, adapita ku Nyumba ya Chauta kukaŵapeza anthuwo. Atayang'ana, adaona mfumu itaima pa nsanja yake pa khomo, atsogoleri ndi anthu oimba malipenga ali pafupi ndi mfumuyo. Anthu onse am'deralo ankakondwa, namaimba malipenga. Anthu oimba nyimbo ali ndi zipangizo zao zoimbira, ndiwo amene ankatsogolera chikondwererocho. Pamenepo Ataliyayo adang'amba zovala zake ndipo mofuula adati, “Akundiwukira! Akundiwukira!” Tsono wansembe Yehoyada adabwera nawo atsogoleri a gulu lankhondo aja naŵauza kuti, “Mtulutseni ameneyu pakati pa mizere mwandandayo. Ndipo aliyense amene amtsate, mumuphe ndi lupanga.” Wansembeyo adaanenadi kuti, “Musamphere m'Nyumba ya Chauta ai.” Choncho anthuwo adamgwira Ataliya uja, ndipo atafika naye ku nyumba ya mfumu, pa khomo lotchedwa la Akavalo, adamuphera pamenepo. Tsono Yehoyada adachititsa chipangano pakati pa iye mwini, ndi anthu onse ndi mfumunso, kuti iwowo akhale anthu akeake a Chauta. Choncho anthu onsewo adapita ku nyumba ya Baala, nakaigwetsa. Maguwa ake ndi mafano ake adaŵaphwanyaphwanya. Kenaka anthuwo adaphanso Matani, wansembe wa Baala, patsogolo pa maguwawo pomwepo. Tsono Yehoyada adaika ansembe a fuko la Levi kuti azilonda Nyumba ya Chauta. Paja Aleviwo Davide adaaŵaika kuti aziyang'anira Nyumba ya Chauta, ndi kumapereka nsembe zopsereza kwa Chauta, monga zidalembedwa m'malamulo a Mose kuti azipereka akukondwa ndipo akumaimba, potsata lamulo la Davide. Iyeyo adaika alonda pa makomo a Nyumba ya Chauta, kuti wina aliyense woipitsidwa pa zachipembedzo asaloŵe. Pambuyo pake adandanditsa atsogoleri, nduna, akazembe a anthu ndi anthu onse am'dzikomo. Onsewo adaperekeza mfumu kuchokera ku Nyumba ya Chauta, nakalowa m'nyumba ya mfumu podzera pa khomo lake lapamwamba; ndipo kumeneko adaikhazika mfumuyo pa mpando waufumu. Motero anthu onse am'dzikomo adakondwa. Ndipo mumzindamo mudakhala bata, Ataliya ataphedwa ndi lupanga. Yowasi anali wa zaka zisanu ndi ziŵiri pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 40 ku Yerusalemu. Mai wake anali Zibiya wa ku Beereseba. Tsono Yowasiyo adachita zolungama pamaso pa Chauta nthaŵi yonse ya moyo wa wansembe Yehoyada. Yehoyada adaipezera mfumuyo akazi aŵiri, ndipo idabereka ana aamuna ndi ana aakazi. Pambuyo pake Yowasi adatsimikiza zokonzanso Nyumba ya Mulungu. Adasonkhanitsa ansembe ndi Alevi, naŵauza kuti, “Pitani ku mizinda ya Yuda, mukasonkhetse ndalama pakati pa Aisraele onse, kuti muzikonzera Nyumba ya Chauta wanu chaka ndi chaka. Muwone kuti zimenezi zichitike mwachangu.” Koma Alevi sadachite zimenezo mofulumira. Motero mfumu idaitana Yehoyada mkulu wa ansembe nimfunsa kuti, “Kodi chifukwa chiyani sudaŵauze Alevi kuti asonkhetse ndalama ku Yuda ndi ku Yerusalemu, ndalama zimene adalamula Mose mtumiki wa Chauta ku mpingo wonse wa Aisraele, ndalama zokonzera hema lamsonkhano?” Paja anthu ake a Ataliya, mkazi woipa uja, adaaonongapo Nyumba ya Mulungu, ndiponso adaatenga zinthu zonse zopatulika za ku Nyumba ya Chautayo, nazipereka kwa Abaala. Motero mfumu idalamula kuti apange bokosi, aliike panja pa khomo la Nyumba ya Chauta. Ndipo adalengeza kwa anthu onse a ku Yuda ndi a mu Yerusalemu, kuti adzapereke kwa Chauta ndalama zimene Mose mtumiki wa Mulungu adaalamula kuchipululu kuja kuti Aisraele onse azipereka. Tsono akalonga onse, pamodzi ndi anthu onse adakondwa, nabwera ndi ndalama zao. Ankaponya ndalamazo m'bokosimo mpaka lidadzaza lonse. Nthaŵi zonse Alevi ankabwera nalo bokosilo kwa nduna zake za mfumu, akaona kuti muli ndalama zambiri. Tsono mlembi wa mfumu pamodzi ndi nduna ya mkulu wa ansembe, ankadzakhuthula ndalamazo, kenaka ankalitenga bokosilo nkulibweza pamalo pake. Umu ndimo m'mene ankachitira tsiku ndi tsiku, mwakuti adasonkha ndalama zambirimbiri. Ndipo mfumu pamodzi ndi Yehoyada ankazipereka kwa akapitao oyang'anira ntchito ya ku Nyumba ya Chauta. Tsono adalemba amisiri omanga ndi miyala ndi amisiri a matabwa, kuti akonzenso Nyumba ya Chauta. Adalembanso amisiri ogwira ntchito ndi chitsulo ndi mkuŵa, kuti akonze Nyumba ya Chauta. Anthu amene adalembedwawo ankagwiradi ntchito, ndipo ntchito yokonzayo idapita m'tsogolo akuigwira ndi manja ao. Choncho anthuwo Nyumba ya Chauta ija adaisandutsanso monga momwe idaaliri kale, ndipo adailimbitsa. Ataimaliza, ndalama zotsala adabwera nazo kwa mfumu ndi kwa Yehoyada. Iwo adapanga ziŵiya za ku Nyumba ya Chauta ndi ndalamazo, ziŵiya zogwirira ntchito ndiponso za nsembe zopsereza. Adapanganso mbale za lubani ndiponso ziŵiya zagolide ndi zasiliva. Anthu ankapereka nsembe zopsereza ku Nyumba ya Chauta kosalekeza, pa nthaŵi yonse ya Yehoyada. Koma Yehoyada adakalamba kwambiri, masiku ake adachuluka, ndipo adamwalira ali wa zaka 130. Adamuika m'manda ku mzinda wa Davide pamodzi ndi mafumu, chifukwa chakuti adaachita zabwino m'dziko la Israele ndipo ankatumikira Mulungu ndi Nyumba yake. Yehoyada atamwalira, akalonga a ku Yuda adabwera kudzalambira mfumu, ndipo mfumu idaŵamvera. Anthu adasiya Nyumba ya Chauta, Mulungu wa makolo ao, namatumikira mafano. Tsono mkwiyo wa Mulungu udagwera anthu a ku Yuda ndi a mu Yerusalemu, chifukwa cha tchimo laoli. Komabe Mulungu adatuma aneneri pakati pao kuti anthuwo aŵabweze kwa Chauta. Koma aneneriwo ataŵadzudzula, anthuwo sadasamaleko ai. Tsono mzimu wa Mulungu udaloŵa mwa Zekariya, mwana wa wansembe Yehoyada. Iye adaimirira pakati pa anthu naŵauza kuti, “Chauta akufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mukuchimwira malamulo a Chauta? Ndithu simudzapindula kanthu?’ ” Koma anthuwo adamchita chiwembu, ndipo mfumu italamula, adamponya miyala m'bwalo la Nyumba ya Chauta. Motero mfumu Yowasi sadakumbukire zabwino zimene Yehoyada bambo wake wa Zekariya adamchitira, koma adapha mwana wake. Ndipo pamene ankafa, mwanayo adati, “Chauta apenye, ndipo abwezere chilango.” Pa kutha kwa chaka, gulu lankhondo la ku Siriya lidadzamenyana ndi Yowasi. Adabwera ku Yuda ndi ku Yerusalemu, napha akazembe onse a anthu pakati pa anthuwo. Ndipo adatumiza zofunkha zao zonse kwa mfumu ya ku Damasiko. Ngakhale gulu lankhondo la ku Siriya lidadza ndi anthu ochepa, Chauta adapereka m'manja mwao gulu lalikulu kwambiri la ankhondo, chifukwa chakuti anthuwo anali atasiya Chauta, Mulungu wa makolo ao. Umu ndimo m'mene anthu a ku Siriya adalangira Yowasi. Asiriya aja atamsiya wovulazidwa kwambiri, anyamata ake adamchita chiwembu, chifukwa cha magazi a mwana wa Yehoyada wansembe uja, ndipo adamphera pabedi pake. Motero iyeyo adafa. Ndipo adamuika m'manda mu mzinda wa Davide, koma sadamuike m'manda a mafumu. Anthu amene adamchita chiwembuwo ndi Zabadi mwana wa Simea Mwamoni, ndi Yehozabadi mwana wa Simeriti Mmowabu. Za ana ake aamuna ndiponso za mau ambiri omtsutsa iyeyo, kudzanso za kumanganso Nyumba ya Chauta, izo zidalembedwa m'buku lofotokoza za mafumu. Ndipo Amaziya mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Amaziya anali wa zaka 25 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 29 ku Yerusalemu. Mai wake anali Yehowadani wa ku Yerusalemu. Tsono adachita zolungama pamaso pa Chauta, komabe osati ndi mtima wangwiro ai. Tsono atangolandira mphamvu zonse zaufumu m'manja mwake, adapha anyamata ake amene adaapha mfumu ija, bambo wake. Koma ana ao sadaŵaphe, potsata zimene zidalembedwa m'malamulo a m'buku la Mose, m'mene Chauta adalamula kuti, “Atate sadzaphedwa chifukwa cha ana ao, kapena ana kuphedwa chifukwa cha atate ao. Koma munthu aliyense adzafera machimo ake.” Tsiku lina Amaziya adasonkhanitsa Ayuda naŵakhazika potsata mabanja ao. Adaŵapatsanso atsogoleri a anthu zikwi ndi a anthu mazana, ku Yuda konse ndi ku Benjamini komwe. Adasonkhanitsa anthu a zaka makumi aŵiri ndi opitirirapo. Anthuwo analipo 300,000, anthu osankhika, okhoza nkhondo, odziŵa kugwira mkondo ndi chishango. Adalembanso anthu ankhondo amphamvu ndi olimba mtima a ku Israele, okwanira 100,000, pa mtengo wa makilogramu 3,400 a siliva. Koma munthu wina wa Mulungu adadza kwa iye, namuuza kuti, “Inu amfumu, musapite ndi gulu lankhondo la ku Israele, pakuti Chauta sali nawo anthu ku Israele, ana a Efuremuŵa. Mukaganiza kuti mudzakhala ndi mphamvu kunkhondoko mwa njira imeneyi, Mulungu adzakugonjetsani pamaso pa adani. Pakuti Mulungu ndiye ali ndi mphamvu za kuthandiza ndi za kugonjetsa.” Amaziya adafunsa munthu wa Mulungu uja kuti, “Koma nanga bwanji za makilogramu a siliva aja amene ndapatsa gulu lankhondo la ku Israele?” Munthu wa Mulunguyo adayankha kuti, “Chauta angathe kukupatsani zambiri kupambana zimenezi.” Pamenepo Amaziya adalichotsa gulu lankhondo la ku Efuremu kuti libwerere kwao. Gulu lankhondolo lidaŵapsera mtima kwambiri anthu a ku Yudawo, ndipo lidapita kwao lili lokwiya kwabasi. Koma Amaziya adalimba mtima, ndipo adaŵatsogolera anthu ake kunka nawo ku Chigwa cha Mchere. Adakaphako anthu okwanira 10,000 a ku Seiri. Anthu a ku Yuda adagwira anthu ena amoyo okwaniranso 10,000. Adakwera nawo pamwamba pa thanthwe, naŵaponya pansi kuchoka pamenepo. Ndiye onsewo adangotekedzeka. Koma gulu lankhondo limene Amaziya adalibweza lija, osalilola kuti lipite nao ku nkhondo, lidakathira nkhondo mizinda ya Yuda kuyambira ku Samariya mpaka ku Betehoroni, naphako anthu okwanira 3,000 ku mizindayo, ndipo adatengako zofunkha zambiri. Tsono Amaziya atabwerako kuja adakapha Aedomuku, adabwera ndi milungu ya anthu a ku Seiri, naiika kuti ikhale milungu yake. Ndipo ankaipembedza ndi kumaifukizira lubani. Nchifukwa chake Chauta adamkwiyira Amaziya. Adatuma mneneri kwa iyeyo, kukamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukufuna milungu ya anthu, imene sidathe kuŵapulumutsa anthuwo m'manja mwanu?” Koma pamene mneneriyo ankalankhula, mfumu ija idamufunsa kuti, “Kodi iweyo tidakuika kuti ukhale phungu wa mfumu? Khala chete! Ufuna kuphedweranji?” Mneneriyo adakhala chete kanthaŵi, kenaka adati, “Ndikudziŵa kuti Mulungu watsimikiza zoti akuwonongeni inu, chifukwa chakuti inuyo mwachita zimenezi osamvera uphungu wanga.” Nthaŵi ina Amaziya, mfumu ya ku Yuda, adachita upo. Adatumiza mau kwa Yehowasi, mwana wa Yehowahazi, mwana wa Yehu, mfumu ya ku Israele, mau omuputa akuti, “Ubwere kuno, udzachione.” Yehowasi, mfumu ya ku Israele, adabweza mau kwa Amaziya, mfumu ya ku Yuda, kuti “Padangotere, mtungwi wa ku Lebanoni udatumiza mau kwa mkungudza wa ku Lebanoni kuti, ‘Pereka mwana wako wamkazi kwa mwana wanga kuti amkwatire.’ Koma chilombo cha ku Lebanoni chidadzera pamenepo nkuupondereza mtungwiwo. Inde, iwe ukuti wagonjetsa Edomu, ndipo tsopano ukudzikuza nkumadzitamira kupambana kwakoko. Koma ai tsono, khala kwanu komweko. Bwanji ukufuna kuutsa mavuto dala? Bwinotu, ungagwe, iweyo pamodzi ndi anthu a ku Yuda!” Koma Amaziya sadasamaleko zimenezi, pakuti ndi Mulungu yemwe adaafuna kuti aŵapereke anthuwo m'manja mwa adani ao, chifukwa chakuti iwowo ankapembedza milungu ya Aedomu. Motero Yehowasi, mfumu ya ku Israele, adapita kukamenyana nkhondo ndi Amaziya mfumu ya ku Yuda ku Betesemesi m'dziko la Yuda. Anthu a ku Yuda adagonjetsedwa ndi a ku Aisraele, ndipo wankhondo aliyense adathaŵira kwao. Tsono ku Betesemesiko Yehowasi, mfumu ya ku Israele, adagwirako Amaziya mfumu ya ku Yuda, mwana wa Yowasi, mdzukulu wa Ahaziya, nabwera naye ku Yerusalemu. Ndipo Yehowasi adagumula khoma la Yerusalemu mamita 200, kuyambira ku chipata cha Efuremu mpaka ku chipata Chapangodya. Pamenepo adalanda golide ndi siliva yense ndi ziŵiya zonse zimene adazipeza m'Nyumba ya Chauta zosungidwa ndi Obededomu. Adatenganso chuma cha ku nyumba ya mfumu, nkugwira anthu ena ngati chikole, nabwerera ku Samariya. Amaziya mwana wa Yowasi, mfumu ya ku Yuda, adakhala moyo zaka 15 atafa Yehowasi, mwana wa Yehowahazi, mfumu ya ku Israele. Tsono ntchito zonse za Amaziya kuyambira pa chiyambi mpaka pomaliza, zidalembedwa m'buku la mafumu a ku Yuda ndi a ku Israele. Kuyambira nthaŵi imene iye adafulatira Chauta, anthu adamchita chiwembu ku Yerusalemu, iyeyo nkuthaŵira ku Lakisi. Koma adaniwo adatuma anzao kuti amlondole ku Lakisiko, ndipo adakamphera komweko. Adamnyamulira pa kavalo, nadzamuika m'manda momwe adaikidwa makolo ake mu mzinda wa Davide. Pambuyo pake anthu onse a ku Yuda adatenga Uziya, wa zaka 16, namlonga ufumu m'malo mwa Amaziya bambo wake. Iyeyo adamanga mzinda wa Eloti naubwezera ku Yuda, mfumu itamwalira. Uziyayo anali wa zaka 16 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 52 ku Yerusalemu. Mai wake anali Yekoliya wa ku Yerusalemu. Adachita zolungama pamaso pa Chauta, monga momwe ankachitira bambo wake Amaziya. Adadzipereka kwa Mulungu pa nthaŵi ya Zekariya amene ankamphunzitsa Uziyayo kuti azilemekeza Mulungu. Ndipo nthaŵi zonse pamene ankadzipereka kwa Chauta, Mulungu ankamupezetsa bwino. Nthaŵi ina Uziya adakamenyana nkhondo ndi Afilisti, nagwetsa linga la Gati ndi la Yabine ndiponso la Asidodi. Kenaka adamanga mizinda m'dziko la Asidodi ndi kwinanso m'dziko la Afilisti. Mulungu adamthandiza pomenyana ndi Afilisti, ndi Arabu amene ankakhala ku Guribaala, ndiponso pomenyana ndi Ameuni. Aamoni ankakhoma msonkho kwa Uziya, ndipo mbiri yake idamveka mpaka ku malire a Ejipito, poti anali wamphamvu kwambiri. Kuwonjezera pamenepo, Uziya adamanga nsanja ku Yerusalemu ku Chipata cha ku Ndonyo, Chipata cha ku Chigwa ndi pa Mphindiko ya linga, ndipo adazilimbitsa. Pambuyo pake adamanga nsanja ku chipululu ndi kukumba zitsime zambiri, poti anali ndi ziŵeto zambiri ku madambo ndi ku zigwa. Analinso ndi anthu olima minda ndi anthu omasamala mphesa ku mapiri, ndiponso ku maiko achonde, poti ankakonda kulima. Komanso Uziyayo anali ndi gulu la asilikali odziŵa nkhondo. Anali m'magulumagulu potsata dongosolo limene adaalikonza mlembi Yeiyele ndi Maaseiya, mkulu wankhondo. Amene ankaŵalamulira asilikaliwo anali Hananiya, mmodzi mwa nduna za mfumu. Chiŵerengero chonse cha atsogoleri amphamvu, olimba mtima, akulu a mabanja, chinali 2,600. Atsogoleri ameneŵa ankalamulira gulu lankhondo lokwanira asilikali 307,500, amene ankatha kumenya nkhondo mwamphamvu, kuthandiza mfumu polimbana ndi adani. Ndipo adapangira asilikaliwo zishango, mikondo, zisoti zankhondo, malaya ankhondo achitsulo, mauta, ndi miyala yoponyera. Ku Yerusalemu anthu aluso adapanga makina amene ankaŵakweza pa nsanja ndi pa malo onse andonyo, kuti anthu aziponyera mivi ndiponso miyala ikuluikulu. Choncho mbiri ya Uziya idamveka nikafika kutali, chifukwa anali atathandizidwa kodabwitsa, mpaka adakhala wamphamvu. Koma Uziyayo mphamvu zake zitachuluka, adayamba kunyada ndipo kunyada kwakeko kudamuwonongetsa. Anali wosakhulupirika kwa Chauta Mulungu wake, ndipo adaloŵa ku Nyumba ya Chauta kuti akafukize lubani pa guwa lofukizapo lubani. Koma wansembe Azariya adaloŵa pambuyo pa iyeyo, pamodzi ndi ansembe a Chauta 80 olimba mtima. Tsono ansembewo adamletsa mfumu Uziya namuuza kuti, “Pepani, mfumu Uziya, sindinu amene muyenera kufukiza lubani kwa Chauta, koma ansembe, ana a Aaroni, amene adaŵapatula kuti azifukiza lubani. Chokaniko ku malo opatulika kwambiriŵa. Kutereku mwalakwa, ndipo ulemerero wa Chauta wakuchokerani.” Apo Uziya adapsa mtima. Tsono m'manja mwake munali chofukizira lubani. Ndipo atakwiyira ansembewo, khate lidatuluka pamphumi pake, ansembe aja akuwona, m'Nyumba ya Chauta, pafupi ndi guwa lofukizirapo lubani. Azariya mkulu wa ansembe, pamodzi ndi ansembe onse atamuyang'ana, adangoona kuti wachita khate pa mphumi. Ansembewo adamkankhira kunja mwamsanga, ndipo iye mwini wake adatuluka msangamsanga, chifukwa chakuti Chauta adaamlanga. Uziya adakhala wakhate mpaka pa tsiku la kufa kwake. Tsono popeza kuti anali wakhate, ankakhala m'nyumba ya yekha, chifukwa anali atachotsedwa ku Nyumba ya Chauta. Motero Yotamu mwana wake ndiye amene ankayang'anira za ku nyumba ya mfumu, namalamulira anthu am'dzikomo. Ntchito zonse za Uziya kuyambira pa chiyambi mpaka pomaliza, adazilemba mneneri Yesaya, mwana wa Amozi. Tsono Uziya adalondola makoko ake ndipo adamuika pamodzi ndi makolo ake ku malo a manda a mafumu, osati m'manda mwaomo, poti anthu ankati, “Iyeyu ndi wakhate.” Ndipo Yotamu mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Yotamu anali wa zaka 25 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 16 ku Yerusalemu. Mai wake anali Yerusa mwana wa Zadoki. Iyeyo adachita zolungama pamaso pa Chauta, kutsata zonse zimene ankachita Uziya, bambo wake, kupatula kuti sadakaloŵe mwamphamvu ku Nyumba ya Chauta. Koma anthu ankachitabe zoipa. Iyeyo adamanga khomo lapamwamba la ku Nyumba ya Chauta, ndipo adagwira ntchito yaikulu yomanga linga la Ofele. Komanso adamanga mizinda ku dziko lonse lamapiri la Yuda. Adamanganso malinga ndi nsanja ku nkhalango zakumapiri. Adamenyana nkhondo ndi mfumu ya Aamoni, ndipo adaŵagonjetsa Aamoniwo. Nchifukwa chake, chaka choyamba Aamoni aja adapereka makilogramu 3,400 a siliva, matani 1,000 a tirigu, ndiponso matani 1,000 a barele. Aamoni ankalipira kwa Yotamuyo zinthu zonga zomwezo pa chaka chachiŵiri ndi chachitatu. Choncho Yotamu adasanduka wamphamvu chifukwa chakuti adasunga makhalidwe oongoka pamaso pa Chauta Mulungu wake. Tsono ntchito zonse za Yotamu, ndi nkhondo zake zonse ndiponso makhalidwe ake, zidalembedwa m'buku la mafumu a ku Israele ndi mafumu a ku Yuda. Iyeyo anali wa zaka 25 pamene ankaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 16 ku Yerusalemu. Pambuyo pake Yotamu adamwalira, naikidwa m'manda mu mzinda wa Davide. Ndipo Ahazi mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Ahazi anali wa zaka 20 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 16 ku Yerusalemu. Iyeyo sadachite zolungama pamaso pa Chauta, monga m'mene ankachitira Davide kholo lake. Koma adatsata zitsanzo za mafumu a ku Israele. Adapanga zifanizo zosungunula za Abaala. Adafukiza lubani ku chigwa cha mwana wa Hinomu, ndipo adapereka ana ake aamuna ngati nsembe yopsereza, potsata miyambo yonyansa ya anthu a mitundu ina imene Chauta adaaipirikitsa m'dzikomo pamene ankafika Aisraele. Ndipo adapereka nsembe, namafukiza lubani ku akachisi opembedzerako mafano, pa mapiri ndi patsinde pa mtengo uliwonse wogudira. Nchifukwa chake Chauta, Mulungu wake, adapereka Ahazi kwa mfumu ya ku Siriya, imene idamgonjetsa. Ndipo anthu ambiri adatengedwa ukapolo kupita ku Damasiko. Chauta adamperekanso Ahaziyo kwa mfumu ya ku Israele, imene idamgonjetsa kotheratu pakupha anthu ambiri. Peka mwana wa Remaliya adaphako anthu okwanira 120,000 a ku Yuda pa tsiku limodzi, chifukwa iwowo adaasiya Chauta, Mulungu wa makolo ao. Onsewo anali anthu olimba mtima. Ndipo Zikiri, munthu wamphamvu wa ku Efuremu, adapha Maaseiya mwana wa mfumu, ndi Azirikamu, nduna ya ku nyumba ya mfumu, ndiponso Elikana, wachiŵiri mu ulamuliro wa mfumu. Anthu a ku Israele adagwira ukapolo abale ao a ku Yuda okwanira 200,000, akazi, ana aamuna, ndi ana aakazi. A ku Israelewo adatenganso zofunkha zambiri kubwera nazo ku Samariya. Koma kumeneko kunali mneneri wina wa Chauta dzina lake Odedi. Iye adapita kuti akakumane ndi gulu lankhondo limene lidadza ku Samariya. Adauza anthuwo kuti, “Popeza kuti Chauta, Mulungu wa makolo anu, adaakwiyira anthu a ku Yuda, adapereka Ayudawo kwa inu. Koma inu mwaŵapha mwaukali, ukali wake wofika mpaka kumwamba. Tsono mukufuna kuti mupondereze anthu a ku Yuda ndi a mu Yerusalemu, amuna ndi akazi omwe, kuti akhale akapolo anu. Kodi inuyo mulibe anu machimo pamaso pa Chauta, Mulungu wanu? Mverani tsono, ndipo muŵabweze akapolo amene mudaŵatenga pakati pa abale anuwo, kuti apite kwao, poti Chauta wakwiya nanu koopsa.” Atsogoleri enanso a anthu a ku Efuremu, monga Azariya mwana wa Yohanani, Berekiya mwana wa Mesilemoti, Yehizikiya mwana wa Salumu, ndi Amasa mwana wa Hadilai, adaimirira kuti amenyane ndi anthu amene ankachoka ku nkhondo. Adaŵauza kuti, “Musati mubwere nawo kuno akapolowo, poti inuyo mukufuna kuti ife tichimwire Chauta kuwonjezera pa machimo athu amene tili nawo, ndiponso kuwonjezera pa zolakwa zathu. Ndithu kulakwa kwathu nkwakukulu ndipo mkwiyo woopsa uli pa Israele.” Motero anthu ankhondo aja adaŵasiya akapolowo, pamodzi ndi zofunkhazo, pamaso pa atsogoleriwo ndi pamaso pa msonkhano wonse. Kenaka anthu amene taŵatchula maina aja, adanyamuka natenga akapolowo. Amene anali maliseche adaŵaveka zovala zimene adaafunkha. Adaŵaveka, naŵapatsa nsapato. Adaŵapatsa zakudya ndi zakumwa. Tsono atanyamula anthu onse ofooka pa abulu, adabwera nawo kwa abale ao ku Yeriko, mzinda wamigwalangwa. Kenaka adabwerera ku Samariya. Pa nthaŵi imeneyo Mfumu Ahazi adatumiza mau kwa mfumu ya ku Asiriya, kupempha chithandizo. Paja Aedomu anali atathiranso nkhondo ku Yuda, ndipo adaagonjetsa Yudayo, natenga anthu kuti akhale akapolo. Afilisti nawonso anali atathira nkhondo mizinda yakuchigwa ndiponso Megebu wa ku Yuda. Ndipo adalanda Betesemesi, Aiyaloni, Gederoti ndiponso Soko pamodzi ndi midzi yake yomwe, Timna pamodzi ndi midzi yake yomwe, ndi Gimizo pamodzi ndi midzi yake yomwe, nakhazikika komweko. Zoonadi Chauta adalitsitsa dziko la Yuda chifukwa cha mfumu Ahazi, popeza kuti adaaipitsa ku Yuda, ndipo anali wosakhulupirika kwa Chauta. Motero Tiligati-Pilinesere, mfumu ya ku Asiriya, adadzamenyana naye nkhondo, ndipo adamvutitsa m'malo momlimbikitsa. Ahazi ankatenga katundu ku Nyumba ya Chauta, ku nyumba ya mfumu ndi ku nyumba za nduna, namakampereka kuti akakhomere msonkho kwa mfumu ya ku Asiriya. Koma zonsezo sizidamthandize. Pa nthaŵi yake yamavutoyo, Ahazi adapitirirabe kukhala wosakhulupirika kwa Chauta. Ankapereka nsembe kwa milungu ya ku Damasiko imene idamgonjetsayo, ndipo ankati, “Chifukwa chakuti milungu ya mafumu a ku Siriya yaŵathandiza iwowo, ine ndidzapereka nsembe kwa milunguyo kuti indithandizenso ine.” Koma milunguyo idamuwononga pamodzi ndi anthu ake onse. Tsono Ahazi adasonkhanitsa ziŵiya za ku Nyumba ya Chauta, naziphwanyaphwanya. Kenaka adatseka zitseko za Nyumba ya Mulungu, nadzimangira maguwa pa malo ambirimbiri mu Yerusalemu. Adamanga akachisi opembedzerako ku mzinda uliwonse wa Yuda, kuti azifukizako lubani kwa milungu ina, kuputa mkwiyo wa Chauta, Mulungu wa makolo ake. Tsono ntchito zonse ndi makhalidwe ake kuyambira pa chiyambi mpaka pomaliza, zidalembedwa m'buku la mafumu a ku Yuda ndi mafumu a ku Israele. Ahazi adamwalira, naikidwa mu mzinda wa Yerusalemu, koma sadamuike m'manda enieni a mafumu. Ndipo Hezekiya mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Hezekiya adamlonga ufumu ali wa zaka 25, ndipo adalamulira zaka 29 ku Yerusalemu. Mai wake anali Abiya, mwana wa Zekariya. Adachita zolungama pamaso pa Chauta monga momwe ankachitira Davide kholo lake. Pa chaka choyamba cha ufumu wake, pa mwezi woyamba, Hezekiya adatsekula zitseko za Nyumba ya Chauta, nazikonza. Adaloŵa ndi ansembe ndi Alevi, naŵasonkhanitsa ku bwalo lakuvuma, ndipo adaŵauza kuti, “Mverani inu Alevi. Mudziyeretse, muyeretsenso Nyumba ya Chauta Mulungu wa makolo anu, pakuchotsa zonyansa ku malo opatulika. Makolo athu adakhala osakhulupirika ndipo adachita zoipa pamaso pa Chauta, Mulungu wathu. Iwo adasiya Chauta, adaloza nkhongo ku malo a Chauta, ndi kumfulatira. Adatsekanso zitseko za khonde la poloŵera, nazima nyale. Sadafukize lubani kapena kupereka nsembe zopsereza ku malo opatulika kwa Mulungu wa Israele. Nchifukwa chake Mulungu adaŵapsera mtima anthu a ku Yuda ndi a mu Yerusalemu. Adaŵasandutsa ochititsa anthu mantha, odabwitsa anthu ndiponso oti anthu aziŵatsonya monga m'mene mukuwoneramu. Makolo athu adaphedwa ndi lupanga, ndipo ana athu aamuna, ana athu aakazi ndi akazi athu ali ku ukapolo chifukwa cha zimenezi. Tsono ine ndikuganiza kuti ndichite chipangano ndi Chauta, Mulungu wa Israele, kuti mkwiyo wake woopsawo utichoke. Ana anga, musachedwe, pakuti Chauta wakusankhani inu kuti muziima pamaso pake ndi kumamtumikira, ndipo kuti mukhale atumiki ake, ndi kumafukiza lubani kwa Iye.” Tsono Alevi amene anali pomwepo ndi aŵa: a m'banja la Kohati: Mahati mwana wa Amasai, ndi Yowele mwana wa Azariya; a m'banja la Merari: Kisi mwana wa Abidi, ndi Azariya mwana wa Yehalelele; a m'banja la Geresoni: Yowa mwana wa Zima, ndi Edeni mwana wa Yowa; a m'banja la Elizafani: Simiri ndi Yeuwele; a banja la Safu: Zekariya ndi Mataniya; a m'banja la Hemani: Yehuwele ndi Simei; a m'banja la Yedutuni: Semaya ndi Uziyele. Iwowo adasonkhanitsa abale ao, ndipo adadziyeretsa, naloŵa m'Nyumba ya Chauta kuti aiyeretse monga momwe mfumu idaalamulira, potsata mau a Chauta. Ansembe ndiwo amene adaaloŵa m'katikati mwa Nyumba ya Mulungu kuti akayeretsemo. Adatulutsa zinthu zonse zonyansa zimene adazipeza m'Nyumbamo, m'bwalo la Nyumbayo. Alevi adazitenga zimenezo, nakazitaya ku mtsinje wa Kidroni. Adayamba mwambo wa kuyeretsa pa tsiku loyamba la mwezi woyamba. Ndipo pa tsiku lachisanu ndi chitatu la mweziwo, mpamene adafika m'khonde la poloŵera m'Nyumba ya Chauta. Tsono adachita mwambo wa kuyeretsa Nyumba ya Chauta ija pa masiku asanu ndi atatu, ndipo adaimaliza pa tsiku la 16 la mwezi woyambawo. Atatha, adapita kwa mfumu Hezekiya nakamuuza kuti, “Tayeretsa Nyumba yonse ya Chauta ija, guwa la nsembe zopsereza, pamodzi ndi zipangizo zake zonse, ndiponso tebulo la buledi wopereka pamaso pa Chauta, pamodzi ndi zipangizo zake zonse. Zipangizo zonse zimene mfumu Ahazi adaazichotsa pamene anali mfumu yosakhulupirika, tazibwezera, ndipo taziyeretsa. Taziika ku guwa la Chauta.” Pambuyo pake mfumu Hezekiya adanyamuka m'mamaŵa, nasonkhanitsa akuluakulu amumzindamo, ndipo adakwera ku Nyumba ya Chauta. Adabwera ndi ng'ombe zamphongo zisanu ndi ziŵiri, nkhosa zamphongo zisanu ndi ziŵiri ndiponso atonde asanu ndi aŵiri kuti aperekere nsembe yopepesera uchimo, kuperekera banja la mfumu, Nyumba ya Chauta ndi Yuda. Ndipo iyeyo adalamula ansembe, ana a Aaroni, kuti azipereke pa guwa la Chauta. Choncho anthuwo adapha ng'ombe zamphongo zija ndipo ansembe adatenga magazi, nawaza pa guwa. Adaphanso nkhosa zamphongo zija, nawaza magazi ake pa guwa. Tsono atonde operekera nsembe yopepesera uchimo aja, adabwera nawo kwa mfumu ndi kwa msonkhano wonse. Ndipo adasanjika manja ao pa atondewo. Kenaka ansembe adazipha, napereka magazi ake pa guwa, kuti akhale mwambo wofafanizira machimo a Aisraele onse, pakuti mfumu idaalamula kuti nsembe yopsereza ndi nsembe zopepesera uchimo zichitike chifukwa cha Aisraele onse. Tsono adaika Alevi kuti azikhala ku Nyumba ya Chauta ndi kumaimba ziwaya zamalipenga, azeze ndi apangwe, potsata lamulo la Davide ndi la Gadi mneneri wa mfumu, ndiponso la Natani mneneri. Pakuti lamulo limenelo nlochokera kwa Chauta kudzera mwa aneneri ake. Alevi adaimirira atatenga zipangizo zoimbira zonga za Davide, ndipo ansembe adatenga malipenga. Pamenepo Hezekiya adalamula kuti nsembe yopsereza iperekedwe pa guwa. Atayamba kupereka nsembe yopsereza, adayambanso kuimbira nyimbo Chauta. Ndipo adaliza malipenga ndi zipangizo zoimbira za Davide mfumu ya Israele. Msonkhano wonse udagwada moŵeramitsa mitu pansi, anthu oimba nyimbo akuimba, ndipo oliza malipenga akuliza. Adakhala akuchita zimenezi mpaka nsembe yopsereza idatha. Atatha kupereka nsembe, mfumu pamodzi ndi anthu onse amene anali nawo adagwada naŵeramitsa mitu pansi. Kenaka mfumu Hezekiya, pamodzi ndi nduna zake, adalamula Alevi kuti aimbe nyimbo zotamanda Chauta potsata mau a Davide ndi a mneneri Asafu. Pomwepo adaimba mosangalala nyimbo zotamanda, ndipo adagwada naŵeramitsa mitu pansi. Pamenepo Hezekiya adati, “Tsopano inu mwadzipereka kuti mugwire ntchito ya Chauta. Idzani pafupi, mubwere nazo nsembe ndi zopereka zothokozera ku Nyumba ya Chauta.” Msonkhanowo udabwera nazo nsembe ndi zopereka zothokozera. Anthu onse amene anali ndi mtima waufulu adabwera ndi nsembe zopsereza. Chiŵerengero cha nsembe zopsereza zimene msonkhano udabwera nazo ndi ichi: ng'ombe zamphongo 70, nkhosa zamphongo 100, ndi anaankhosa 200. Zonsezi adazipereka ngati nsembe yopsereza kwa Chauta. Tsono nsembe zina zopereka zinali izi: ng'ombe zamphongo 600 ndi nkhosa 300. Koma ansembe anali pang'ono, choncho sadathe kusenda nsembe zonse zopserezazo. Motero poyembekeza kuti ansembe onse adziyeretse, Alevi adaŵathandiza mpaka ntchito yonseyo idatha. Aleviwo adaachita changu kupambana ansembe pakudziyeretsa kwao. Kuwonjezera pa chiŵerengero cha nsembe zopsereza, panalinso mafuta a nsembe zamtendere, ndiponso zakumwa za pa nsembe zopsereza. Motero miyambo yonse ya ku Nyumba ya Chauta idakhazikikanso. Choncho Hezekiya ndi anthu onse aja adakondwa chifukwa cha zimene Mulungu adaŵachitira, pakuti zimenezo zidaachitika mwadzidzidzi. Hezekiya adatumiza mau ku Israele konse ndi ku Yuda, ndipo adalembanso makalata kwa Aefuremu ndi kwa Amanase kuti, “Mubwere ku Nyumba ya Chauta ku Yerusalemu, kudzachita mwambo wa Paska ya Chauta, Mulungu wa Israele. Pakuti mfumu, nduna zake ndi anthu onse a ku Yerusalemu anali atapangana kuti azichita Paska pa mwezi wachiŵiri. Zidaatero chifukwa sankatha kuchita Paskayo pa nthaŵi yake, popeza kuti ansembe oyeretsedwa anali osakwanira, ndipo anthu nawonso anali asanasonkhane ku Yerusalemu. Zimenezi zidakomera mfumu ndi msonkhano wonse. Choncho anthuwo adatsimikiza zoti alengeze ku Israele konse, kuyambira ku Beereseba mpaka ku Dani, kuti anthu abwere kudzachita Paska ya Chauta, Mulungu wa Israele, ku Yerusalemu, pakuti si ambiri ankachita Paskayo monga kudaalembedwera. Motero amithenga adapita ku Israele konse ndi ku Yuda, atatenga makalata a mfumu ndi a nduna zake. Makalatawo ankanena kuti, ‘Inu Aisraele, bwererani kwa Chauta, Mulungu wa Abrahamu, Isaki ndi Israele, kuti Iyeyo abwerenso kwa otsalanu, amene mudapulumuka kwa mafumu a ku Asiriya. Musati mukhale ngati makolo anu ndi abale anu amene sadakhulupirire Chauta, Mulungu wa makolo ao, kotero kuti adaŵaononga monga momwe mukuwoneramu. Musati muumitse makosi anu monga m'mene ankachitira makolo anu, koma mudzipereke kwa Chauta, ndipo muzibwera ku Nyumba yake imene Chautayo waiyeretsa mpaka muyaya. Ndipo muzitumikira Chauta, Mulungu wanu, kuti mkwiyo wake woopsa ukuchokeni. Chifukwatu ngati inu mubwerera kwa Chauta, anthu amene adagwira ukapolo abale anu ndi ana anu, adzachita chifundo, ndipo abale anuwo adzabweranso ku dziko lino. Paja Chauta, Mulungu wanu, ndi wokoma mtima ndi wachifundo, ndipo sadzakufulatirani ngati mubwerera kwa Iyeyo.’ ” Choncho amithenga aja adapita ku mzinda uliwonse m'dziko lonse la Efuremu ndiponso m'dziko lonse la Manase mpaka kukafika ku Zebuloni. Koma anthu ankaŵaseka monyodola nkumaŵalalatira. Anthu pang'ono chabe a ku Asere ndi a ku Manase ndiponso a ku Zebuloni adadzichepetsa napita ku Yerusalemu. Dzanja la Mulungu linalinso ndi anthu a ku Yuda, kuti aŵapatse mtima umodzi wochita zimene mfumu ndi nduna zake adaalamula, monga momwe Chauta adaanenera. Choncho anthu ambiri adabwera ku Yerusalemu kudzachita chikondwerero cha buledi wosafufumitsa pa mwezi wachiŵiri. Unali msonkhano waukulu kwambiri. Anthuwo adayambapo kumagwira ntchito, ndipo ku Yerusalemuko adachotsa maguwa operekapo nsembe ndi ena ofukizirapo lubani, nakaŵataya ku chigwa cha Kidroni. Ndipo adapha mwanawankhosa wa Paska pa mwezi wachiŵiri. Choncho ansembe ndi Alevi adachita manyazi, kotero kuti adadziyeretsa, nabwera ndi nsembe zopsereza ku Nyumba ya Chauta. Adakhala m'malo mwao potsata lamulo la Mose, munthu wa Mulungu uja. Ansembewo adawaza magazi amene adalandira kwa Alevi. Pakuti mumsonkhanomo munali anthu ambiri amene sadadziyeretse, Alevi ndiwo adayenera kupha mwanawankhosa wa Paska wa munthu aliyense amene anali woipitsidwa pa zachipembedzo, kuti aiyeretse nsembeyo pamaso pa Chauta. Ndiye kuti chinamtindi cha anthu, ambiri mwa iwo a ku Efuremu, a ku Manase, a ku Isakara ndi a ku Zebuloni, anali oipitsidwa pa zachipembedzo. Koma adadya naobe Paska, monyozera mwambo wolamulidwa. Koma Hezekiya adaaŵapempherera kuti, “Chauta, Mulungu wabwino, mukhululukire munthu aliyense amene amaika mtima pa kufunafuna Mulungu, Chauta, Mulungu wa makolo ake, ngakhale kuti munthuyo sadatsate malamulo onena za kuyeretsedwa koyenera Nyumba ya Chauta.” Ndipo Chauta adamvera Hezekiya naŵachiritsa anthuwo. Tsono anthu a ku Israele amene analipo ku Yerusalemu kuja, adachita chikondwerero cha buledi wosafufumitsa masiku asanu ndi aŵiri, ndipo adasangalala kwambiri. Alevi pamodzi ndi ansembe ankatamanda Chauta tsiku ndi tsiku, akumuimbira ndi mphamvu zao zonse. Tsono Hezekiya adalankhula moŵalimbitsa mtima Alevi onse ogwira ntchito ya Chauta mwaluso. Choncho anthuwo adachita chikondwerero masiku asanu ndi aŵiri, napereka nsembe zachiyanjano ndi kuthokoza Chauta, Mulungu wa makolo ao. Pambuyo pake msonkhano wonse udavomerezana zopitiriza chikondwererocho masiku asanu ndi aŵiri ena. Choncho adachitadi chikondwerero masiku asanu ndi aŵiri ena mosangalala. Hezekiya mfumu ya ku Yuda adaapereka ng'ombe zamphongo 1,000 ku msonkhanowo, ndiponso nkhosa 7,000 zoyenera kuzipereka ku nsembe. Nduna zake zidaperekanso ng'ombe zamphongo 1,000 ndi nkhosa 10,000. Ansembe ambirimbiri adadziyeretsa. Msonkhano wonse wa ku Yuda, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi, gulu lonse la anthu amene adaachokera ku Israele, alendo ongokhala nao amene adaachokera ku dziko la Israele, ndiponso alendo ongokhala nao a ku dziko la Yuda, onsewo adakondwa. Choncho kunali chikondwerero chachikulu ku Yerusalemu, pakuti kuyambira nthaŵi ya Solomoni, mwana wa Davide, mfumu ya Israele, sizidachitikepo zotere ku Yerusalemu. Tsono ansembe pamodzi ndi Alevi adaimirira nadalitsa anthu. Mau ao adamveka, ndipo pemphero lao lidakafika ku malo oyera a Mulungu kumwamba. Zonsezi zitatha, Aisraele onse amene analipo adapita ku mizinda ya Yuda, nakaphwanyaphwanya zipilala, kugwetsa mafano, ndi kuwononga akachisi ndiponso maguwa ku dziko lonse la Yuda, Benjamini, Efuremu ndi Manase, mpaka kuwonongeratu zonse. Pambuyo pake Aisraele onse adabwereranso kumapita kumizinda kwao, aliyense ku dziko lake. Hezekiya adakhazikitsanso magulu a ansembe ndi a Alevi, gulu lililonse kutsata ntchito yake. Ansembe ndi Aleviwo ena adaŵaika kuti azipereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, ena kumatumikira ku zipata za bwalo la Chauta, ena kumathokoza ndi kutamanda. Mfumu idapatula chigawo cha chuma chake, kuti zipezeke nsembe zopsereza izi: zam'maŵa, zamadzulo, za masiku a Sabata, za pachiyambi pa mwezi ndiponso za masiku a chikondwerero okhazikitsidwa, monga momwe zidalembedwera m'malamulo a Chauta. Ndipo adalamula anthu a ku Yerusalemu kuti azipereka chigawo choyenera ansembe ndi Alevi, kuti pakutero ansembe ndi Aleviwo azidzipereka ku malamulo a Chauta. Tsono lamulo limenelo atangolilengeza, pomwepo Aisraele adayamba kupereka kwambiri zipatso zoyamba kucha za tirigu, vinyo, mafuta, uchi ndi zonse zam'minda. Adabweranso ndi zachikhumi zambirimbiri za zinthu zonse. Aisraele ndi Ayuda amene ankakhala ku mizinda ya Yuda, ankabwera ndi zigawo zachikhumi za ng'ombe ndi nkhosa, ndiponso zinthu zopatulika zimene anali atazipereka kwa Chauta, Mulungu wao, namaziika zonsezo m'milum'milu. Adayamba kumaunjika milu pa mwezi wachitatu natsiriza pa mwezi wachisanu ndi chiŵiri. Tsono Hezekiya ndi nduna zake atabwera naona miluyo, adatamanda Chauta pamodzi ndi Aisraele anthu ao. Hezekiyayo adafunsa ansembe ndi Alevi za milu ija. Azariya mkulu wa ansembe amene anali wa m'banja la Zadoki, adamuyankha kuti, “Chiyambire chake cha kupereka zopereka zao ku Nyumba ya Chauta, takhala ndi zinthu zambiri zakudya, ndipo zotsalanso nzambiri. Pakutitu Chauta wadalitsa anthuwo, kotero kuti tili nazo zambirimbiri zotsalazi.” Tsono Hezekiya adaŵalamula anthuwo kuti akonze zipinda za ku Nyumba ya Chauta. Iwo adakonzadi zipindazo. Pambuyo pake adabwera nazo zoperekazo mokhulupirika, zigawo zachikhumi ndiponso zinthu zopatulika. Tsono kapitao wamkulu woŵayang'anira anali Konaniya Mlevi, pamodzi ndi Simei mbale wake, amene anali wachiŵiri. Yehiyele, Azariya, Nahati, Asahele, Yerimoti, Yozabadi, Eliyele, Isiimakiya, Mahati, ndi Benaya, ndiwo amene anali akapitao othandiza Konaniya ndi Simei mbale wake. Mfumu Hezekiya ndiye amene adaŵasankha, pamodzi ndi Azariya amene anali kapitao wamkulu wa ku Nyumba ya Chauta. Ndipo Kore, mwana wa Imina Mlevi, amene ankalonda pa chipata chakuvuma ndiye ankayang'anira nsembe zaulere zopereka kwa Mulungu. Ankapatula chigawo cha zopereka choyenera Chauta ndiponso zopereka zoyera kopambana. Edeni, Miniyamini, Yesuwa, Semaya, Amariya ndi Sekaniya, ndiwo amene ankamthandiza mokhulupirika ku mizinda ya ansembe, popereka magawo a zopereka kwa abale ao, akuluakulu ndi ang'onoang'ono omwe, molingana ndi magulu ao. Komanso ankapereka kwa anthu olembedwa potsata mabanja a anthu, ndiye kuti amuna kuyambira a zaka makumi atatu mpaka kupitirirapo, amene ankaloŵa m'Nyumba ya Chauta kuti azigwira ntchito yofunika pa tsiku lake, malinga ndi nthaŵi yao ndi magulu ao. Ansembe ankaŵalemba potsata mabanja a makolo ao. Alevi ankaŵalemba kuyambira anthu a zaka makumi aŵiri ndi opitirirapo, potsata mtundu wa ntchito yao ndi magulu ao. Ansembe adalembedwa pamodzi ndi ana ao onse akhanda, akazi ao, ana ao aamuna ndi aakazi, kungoti onse a m'banja mwao, chifukwa anali oyenera kudziyeretsa mokhulupirika. Kunena za ansembe, ana a Aaroni amene ankakhala ku madera okhala ndi mabusa a mizinda yao, panali amuna ena m'mizinda yoŵerengeka, amene adaauzidwa pakuŵatchula maina, kuti azipereka magawo a chakudya kwa munthu wamwamuna aliyense pakati pa ansembewo, ndiponso kwa aliyense pakati pa Alevi amene adalembedwa. Hezekiya adachita zimenezi ku dziko lonse la Yuda. Motero adachita zabwino, zolungama ndi zokhulupirika pamaso pa Chauta, Mulungu wake. Ntchito iliyonse imene ankachita potumikira ku Nyumba ya Chauta potsata malangizo ndi malamulo, ndi pofunafuna Mulungu wake, ankachita zimenezo ndi mtima wake wonse ndipo ankapeza mwai. Pambuyo pake, zitatha ntchito zachikhulupirirozi, Senakeribu, mfumu ya ku Asiriya, adabwera kudzathira nkhondo dziko la Yuda, ndipo adamanga zithando zankhondo kuzinga mizinda yamalinga. Ankati aŵagumule malinga akewo. Hezekiya ataona kuti Senakeribu wabwera, ndipo akufuna kuthira nkhondo Yerusalemu, adapangana ndi nduna zake pamodzi ndi atsogoleri a gulu lankhondo, kuti akatseke madzi a ku akasupe kunja kwa mzindawo. Anthuwo adamthandiza, ndipo anthu ambiri adasonkhana kuti atseke akasupe onse pamodzi ndi mfuleni womwe umene unkayenda m'kati mwa nthakamo. Iwo ankati, “Akafika kuno mafumu a ku Asiriya, adzapezerenji madzi ambiri?” Hezekiya adalimba mtima, nayamba kumanganso khoma limene linali litagamuka. Tsono adamanganso nsanja pakhomapo, ndiponso ina kunja kwake. Adalimbitsanso linga lotchedwa Milo ku mzinda wa Davide. Adapanga zida zankhondo ndi zishango zambirimbiri. Tsono adaika atsogoleri ankhondo kuti azilamula anthu, naŵasonkhanitsa anthuwo pa bwalo ku chipata cha mzindawo. Tsono adaŵalankhula moŵalimbitsa mtima kuti, “Khalani amphamvu, limbani mtima. Musati muwope kapena kutaya mtima pamaso pa mfumu ya ku Asiriya ndi chigulu chankhondo chimene ali nachochi. Iyeyo ali ndi gulu lankhondo la anthu, koma ife tili ndi Chauta, Mulungu wathu, wotithandiza ndi wotimenyera nkhondo zathu.” Apo anthuwo adakhulupirira mau a Hezekiya mfumu ya ku Yuda. Pambuyo pa zimenezi Senakeribu, mfumu ya ku Asiriya, amene anali atazinga mzinda wa Lakisi pamodzi ndi ankhondo ake onse, adatuma akazembe ake ku Yerusalemu kwa Hezekiya mfumu ya ku Yuda ndi kwa anthu onse a ku Yuda amene anali mu Yerusalemu. Adaŵatuma ndi mau akuti, “Senakeribu, mfumu ya ku Asiriya, akufunsa kuti, ‘Kodi mukukhulupirira chiyani, kuti muzikanirira mu Yerusalemu ndi kumatsekedwa? Kodi Hezekiya sakukulakwitsani, kuti akuphetseni ndi njala ndi ludzu, pamene akukuuzani kuti, “Chauta, Mulungu wathu, adzatipulumutsa kwa mfumu ya ku Asiriya?” Kodi si Hezekiya yemweyu amene adachotsa akachisi ndi maguwa ku mapiri, nalamula anthu a ku Yuda ndi a mu Yerusalemu kuti, “Muzipembedza ku guwa limodzi lokha ndipo muzipereka nsembe zanu zopsereza pa guwa limodzi lokhalo?” Kodi inu simukudziŵa zimene ine ndi makolo anga takhala tikuichita mitundu yonse ya anthu a maiko ena? Kodi milungu ya mitundu ina ya anthu a m'maikowo idatha kupulumutsa maiko ao m'manja mwanga? Kodi pakati pa milungu ya mitundu ina ya anthuyo, imene makolo anga adaiwononga kotheratu, ndi uti amene adatha kupulumutsa anthu ake m'manja mwanga, kuti inuyo muziti Mulungu wanu adzakupulumutsani m'manja mwanga? Ndiye inutu tsono, musalole kuti Hezekiya akunyengeni kapena kukusokezani motero ai, ndipo musamkhulupirire. Chifukwa palibe mulungu wa mtundu kapena ufumu wina uliwonse amene adatha kuŵapulumutsa anthu ake m'manja mwanga kapena m'manja mwa makolo anga. Mulungu wanuyo sadzatha kukupulumutsani m'manja mwanga ai.’ ” Akazembe akewo ankalankhula zambiri zonyoza Ambuye Chauta ndi mtumiki wake Hezekiya. Kenaka Senakeribu adalemba makalata achipongwe oputa Chauta, Mulungu wa Aisraele, adati, “Monga milungu ya mitundu ina ya anthu a m'maiko ena sidathe kuŵapulumutsa anthu ao m'manja mwanga, momwemonso Mulungu wa Hezekiya sadzatha kupulumutsa anthu ake m'manja mwanga.” Ndipo anthuwo mofuula adalengeza zimenezi m'chilankhulo cha Chiyuda kwa anthu a mu Yerusalemu amene anali pa khoma, kuti aŵachititse mantha ndi kuŵaopsa, ndi cholinga choti alande mzindawo. Ankalankhula za Mulungu wa ku Yerusalemu monga momwe ankalankhulira za milungu ya mitundu ina ya anthu a pa dziko lapansi, imene ili milungu yopangidwa ndi manja a anthu. Pamenepo mfumu Hezekiya pamodzi ndi mneneri Yesaya mwana wa Amozi, adayamba kupemphera, nafuulira kumwamba. Tsono Chauta adatuma mngelo, ndipo iye adadzapha ankhondo onse amphamvu, atsogoleri ndi akulu a ku zithando za mfumu ya ku Asiriya. Choncho Senakeribu adabwerera kumapita ku dziko la kwao ali ndi nkhope yamanyazi. Ndipo atakaloŵa m'nyumba ya Chauta wake, ana ake ena adamupha momwemo ndi lupanga. Choncho Chauta adapulumutsa Hezekiya, pamodzi ndi anthu onse amene ankakhala mu Yerusalemu, kwa Senakeribu, mfumu ya ku Asiriya, ndiponso kwa adani ao onse. Motero Chautayo ankaŵatchinjiriza anthuwo konsekonse. Tsono anthu ambiri adabwera ndi zopereka kwa Chauta ku Yerusalemu, nadzaperekanso mphatso kwa Hezekiya mfumu ya ku Yuda. Zitachitika zimenezo, Hezekiyayo adakhala wolemekezeka kwambiri pamaso pa mitundu yonse ya anthu, kuyambira nthaŵi imeneyo mpaka m'tsogolo. Pa nthaŵi imeneyo Hezekiya adadwala, ndipo anali pafupi kufa, tsono adapemphera kwa Chauta, ndipo Chautayo adamuyankha, nampatsa chizindikiro chakuti adzachira. Koma Hezekiya sadachite molingana ndi zabwino zimene Chauta adaamchitira, poti mtima wake unali wodzitama. Nchifukwa chake mkwiyo wa Chauta udamugwera iyeyo, ndiponso anthu a ku Yuda ndi a mu Yerusalemu. Koma kenaka Hezekiya adadzichepetsa naleka kudzikuza, iyeyo ndi anthu amene ankakhala mu Yerusalemu. Motero mkwiyo wa Chauta sudagwe pa anthuwo pa masiku a Hezekiya. Hezekiya anali wolemera kwambiri ndiponso waulemu zedi. Tsono adadzimangira nyumba zomasungiramo chuma cha siliva, golide, miyala yamtengowapatali, zonunkhira, zishango ndiponso mitundu yonse ya ziŵiya zamtengowapatali. Adamanganso nyumba zosungiramo tirigu, vinyo ndi mafuta. Adamanga makola a mitundu yonse ya ziŵeto zosiyanasiyana ndi makola a nkhosa. Komanso adamanga mizinda yake, ndipo anali ndi nkhosa ndi ng'ombe zambirimbiri, pakuti Mulungu adaamlemeza kwambiri. Hezekiyayu ndiye amene adaatseka ngalande yakumtunda ya madzi a ku Gihoni, nkuŵaongolera kuti atsikire kuzambwe kwa mzinda wa Davide. Ankakhoza pa ntchito zonse zimene ankachita. Choncho pamene amithenga a nduna za ku Babiloni adatumidwa kwa Hezekiya kuti akafunse za chizindikiro chija chimene chidachitika m'dzikomo, Mulungu adamsiya yekha, kuti amuyese ndipo kuti adziŵe zonse za mumtima mwake. Tsono ntchito zonse za Hezekiya, pamodzi ndi zabwino zimene ankachita, zidalembedwa m'nkhani yosimba za zimene Yesaya mneneri mwana wa Amozi adaziwona m'masomphenya. Nkhani imeneyi idalembedwa m'buku la mafumu a ku Yuda ndi a ku Israele. Hezekiya adamwalira, naikidwa ku chikwera ku manda a ana a Davide. Anthu onse a ku Yuda pamodzi ndi a mu Yerusalemu adamchitira ulemu pa maliro ake. Tsono Manase mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Manase anali wa zaka khumi ndi ziŵiri pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 55 ku Yerusalemu. Iyeyu adachita zoipa pamaso pa Chauta potsata ntchito zonyansa za anthu a mitundu ina, amene Chauta adaaŵapirikitsa pofika Aisraele. Adayambitsanso akachisi amene bambo wake Hezekiya adaaŵaononga. Adapanganso maguwa a Abaala ndiponso mafano, namapembedza zinthu zonse zamumlengalenga, ndi kumazitumikira. Adamanga maguwa achikunja m'Nyumba ya Chauta imene Chauta mwini wake anali atanena kuti, “Dzina langa lidzakhala ku Yerusalemu mpaka muyaya.” Adamanga maguwa m'mabwalo aŵiri a Nyumba ya Chauta, kumangira zolengedwa zonse zamumlengalenga. Ndipo adapereka ana ake aamuna ngati nsembe yopsereza. Adachita zimenezi ku chigwa cha mwana wa Hinomu, ndipo ankachita zobwebwetetsa, namasamala zamalodza ndi zanyanga, nkumamvana ndi anthu olankhula ndi mizimu ndi anthu amatsenga. Adachita zoipa zambiri pamaso pa Chauta, naputa mkwiyo wake. Tsono m'Nyumba ya Chauta adaikamo fano lopanga iyeyo, Nyumba imene Mulungu adaauza Davide ndi Solomoni mwana wake kuti, “M'nyumba imeneyi, mu Yerusalemu muno, malo amene ndaŵasankhula pakati pa mafuko onse a Aisraele, ndimo m'mene adzatamandira dzina langa mpaka muyaya. Ndipo sindidzachotsa phazi la Israele m'dziko limene ndidapatsa makolo anu, pokhapokha akamasamala ndi kuchita zonse zimene ndidaŵauza pakumvera malamulo ndi malangizo onse amene ndidaŵapatsa kudzera mwa Mose.” Manase adachimwitsa anthu a ku Yuda pamodzi ndi anthu okhala mu Yerusalemu. Ankachita zoipa zambiri kupambana anthu a mitundu ina amene Chauta adaŵaononga pofika Aisraele. Chauta adalankhula ndi Manase ndiponso ndi anthu ake, koma iwo sadasamaleko. Nchifukwa chake Chautayo adaŵatumira atsogoleri ankhondo a mfumu ya ku Asiriya kudzamenyana naye Manase. Adamkoka ndi ngowe zachitsulo nammanga ndi maunyolo amkuŵa, nkupita naye ku Babiloni. Ndiye pamene anali pa mavuto, adapempha kuti Chauta, Mulungu wake, amkomere mtima, ndipo adadzichepetsa kwambiri pamaso pa Mulungu wa makolo ake. Atapemphera kwa Iye, Mulungu adamva kupempha kwake ndi kupemba kwake, ndipo adambwezanso ku Yerusalemu mu ufumu wake. Motero Manase adadziŵa kuti Chauta ndi Mulungu. Pambuyo pake adamanga khoma la kunja kwa mzinda wa Davide kuzambwe kwake kwa Gihoni, kuchokera ku chigwa mpaka poloŵera ku Chipata cha Nsomba. Ndipo adamanga khomalo kuzungulira Ofele nalikweza kwambiri. Adaikanso atsogoleri ankhondo ku mizinda yonse yamalinga ya ku Yuda. Adachotsa milungu yachilendo ndiponso fano m'Nyumba ya Mulungu. Adachotsa maguwa onse achikunja amene anali ataŵamanga pa phiri la Chauta ku Yerusalemu. Ndipo adaŵataya kunja kwa mzinda. Adamanganso guwa la Chauta, namaperekerapo nsembe zachiyanjano ndiponso nsembe zothokozera. Tsono adalamula anthu a ku Yuda kuti azitumikira Chauta Mulungu wa Israele. Anthuwo ankaperekabe nsembe ku akachisi, koma kwa Chauta, Mulungu wao yekha. Tsono ntchito zina zonse za Manase, pamodzi ndi pemphero lake kwa Mulungu wake, ndiponso mau a aneneri amene adalankhula naye m'dzina la Chauta, Mulungu wa Israele, zidalembedwa m'buku la mbiri ya mafumu a ku Israele. Ndipo pemphero lake ndi m'mene Mulungu adalilandirira pemphero lakelo, machimo ake onse, kusakhulupirika kwake, akachisi amene adayambitsa, m'mene adakhazikitsira mafano ndi zithunzi zina, asanadzichepetse paja, zonsezi zidalembedwa m'buku la mbiri ya aneneri. Choncho Manase adamwalira, naikidwa m'nyumba mwake. Tsono Amoni mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Amoni anali wa zaka 22 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka ziŵiri ku Yerusalemu. Iyeyo adachita zoipa pamaso pa Chauta monga m'mene ankachitira Manase bambo wake. Amoniyo ankapereka nsembe kwa mafano onse amene bambo wake adaŵapanga, ndipo ankaŵatumikira. Sadadzichepetse pamaso pa Chauta monga momwe Manase bambo wake adadzichepetsera. Koma Amoniyu ankadzipereka ku machimo kosalekeza. Tsono anyamata ake adamchita chiwembu, namupha m'nyumba mwake. Koma anthu am'dzikomo adapha onse aja amene adamchita chiwembu Amoniyo. Kenaka anthuwo adalonga Yosiya mwana wake kuti akhale mfumu m'malo mwake. Yosiya anali wa zaka zisanu ndi zitatu pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 31 ku Yerusalemu. Iyeyo adachita zolungama pamaso pa Chauta, namatsata chitsanzo cha Davide kholo lake pa zonse, osapatukira kumanja kapena kumanzere. Pa chaka chachisanu ndi chitatu cha ufumu wake, adakali mnyamata, adayambapo kumapembedza Mulungu wa Davide kholo lake. Ndipo pa chaka cha 12 adayamba kuchotsa akachisi opembedzerako mafano ku Yuda ndi mu Yerusalemu. Adachotsanso mafano, osema ndi osungunula. Anthu adagumula maguwa a Abaala, iyeyo ali pomwepo. Adagwetsa maguwa ofukizirapo lubani, ndiponso mafano a dzuŵa amene ankakhala pamwamba pake, adaŵagwetsa pansi. Adaphwanya mafano, osema ndi osungunula. Tsono adaŵaperapera mpaka kuŵasandutsa fumbi, ndipo adawaza fumbilo pa manda a anthu amene ankapereka nsembe kwa mafano. Iyeyo adatenthanso mafupa a ansembe ao pa maguwa ao ndipo adayeretsa dziko la Yuda ndi mzinda wa Yerusalemu. Adayeretsanso mizinda ya Manase, Efuremu, Simeoni, mpaka ku Nafutali, kudzanso mabwinja ao oŵazungulira. Adagwetsamo maguwa, naphwanyaphwanya mafano ndi zithunzi, mpaka kuzidyukula ngati fumbi. Ndipo adagwetsa maguwa ofukizirapo lubani m'dziko lonse la Israele. Pambuyo pake adabwerera ku Yerusalemu. Pa chaka cha 18 cha ufumu wake, atayeretsa dzikolo pamodzi ndi Nyumba ya Chauta yomwe, Yosiya adatuma Safani, mwana wa Azaliya, ndi Maaseiya, kazembe wa mzinda, kudzanso Yowa, mwana wa Yowahazi, mlembi wolemba mbiri, kuti akonze Nyumba ya Chauta Mulungu wake. Iwoŵa adadza kwa Hilikiya mkulu wa ansembe, napereka ndalama zimene adaabwera nazo ku Nyumba ya Chauta. Ndalamazo nzimene Alevi ndi alonda apakhomo adaasonkha ku dziko la Manase ndi la Efuremu ndi kwa anthu onse otsala a ku Israele, kwa onse a ku Yuda ndi a ku Benjamini ndiponso kwa nzika zonse za mu Yerusalemu. Iwowo adapereka ndalamazo kwa akapitao oyang'anira Nyumba ya Chauta. Adaperekako ndalama zina kwa anthu ogwira ntchito ku Nyumba ya Chauta, kuti aikonze ndi kuilimbitsa. Adaperekanso ndalama zina kwa amisiri amatabwa ndi kwa amisiri omanga nyumba, kuti agule miyala yosema ndi mitengo ya mitanda ndi phaso la nyumba, zimene mafumu a ku Yuda adaalola kuti ziwonongeke. Anthuwo adagwira ntchitoyo mokhulupirika. Amene ankaŵayang'anira anali Yahati ndi Obadiya, a m'banja la Alevi, ana a Merari. Zekariya ndi Mesulamu, ana aamuna a m'banja la Akohati, adaŵaikamo kuti aziyang'anira. Alevi onse amene anali ndi luso la kumaimba ndi zipangizo zoimbira, ankayang'anira anthu onyamula katundu, namatsogolera anthu onse amene ankagwira ntchito iliyonse yotumikira. Alevi ena anali alembi, akapitao ndiponso alonda apamakomo. Pa nthaŵi imene ankatulutsa ndalama zimene adaabwera nazo ku Nyumba ya Chauta, wansembe Hilikiya adapeza buku la Malamulo a Chauta, Malamulo aja amene Mulungu adaaŵapereka kudzera mwa Mose. Pomwepo Hilikiyayo adauza Safani mlembi kuti, “Ndalipeza buku la Malamulo lija m'Nyumba ya Chauta.” Ndipo adapereka bukulo kwa Safani. Safani adadza nalo kwa mfumu, ndiponso adauza mfumu kuti, “Zonse zimene mudauza atumiki anu kuti achite, akuchita. Akhuthula ndalama zimene zinali m'Nyumba ya Chauta, azipereka kwa akapitao ndi kwa antchito.” Tsono Safaniyo adauza mfumu kuti, “Wansembe Hilikiya wandipatsira buku.” Ndipo adaliŵerenga bukulo pamaso pa mfumu. Mfumu itamva mau a Malamulo, idang'amba zovala zake mwachisoni. Pomwepo idalamula Hilikiya, Ahikamu mwana wa Safani, Abidoni mwana wa Mika, Safani mlembi uja ndi Asaya mtumiki wa mfumu kuti, “Pitani, mukafunse kwa Chauta m'malo mwanga ndi m'malo mwa anthu otsala ku Israele ndi ku Yuda, za mau a m'buku limene lapezekali. Ndithu mkwiyo wa Chauta umene watiyakirawu ngwaukulu, chifukwa choti makolo athu sadamvere mau a Chauta, sadatsate zonse zimene zalembedwa m'bukuli.” Choncho Hilikiya, pamodzi ndi anthu amene mfumu idaŵatuma aja, adapita kwa mneneri wamkazi dzina lake Hulida, mkazi wa Salumu. Salumuyo, wosunga zovala zachifumu, anali mwana wa Tokati, mwana wa Hasira. Mkaziyo ankakhala ku Yerusalemu m'dera lachiŵiri la mzindawo. Tsono anthu aja atalankhula naye adamuuza za nkhaniyo, Iyeyo adaŵauza kuti, “Chauta, Mulungu wa Israele, akunena kuti, Muuzeni munthu amene wakutumani kwa Ineyo kuti, Ine Chauta ndikuti, Ndidzabweretsa choipa ku mzinda uno ndi pa anthu onse am'menemo, potsata matemberero onse olembedwa m'buku limene adaliŵerenga pamaso pa mfumu ya ku Yuda. Chifukwa chakuti anthuwo adandisiya Ine namapembedza milungu ina, nkumandichimwira ndi mafano ao, adaputa mkwiyo wanga ndi ntchito zonse za manja ao, Ine pano mkwiyo wanga wayakira mzinda uno, ndipo sudzazima ai. Koma mfumu ya ku Yuda imene idakutumani kuti mukafunse Chauta, mukaiwuze kuti Ine Chauta, Mulungu wa Aisraele, ndikuti, Kumva wamva ndithu, pakuti mtima wako walapa ndipo wadzichepetsa pamaso pa Mulungu, utamva mau ake otsutsa mzinda uno ndi anthu onse am'menemo. Popeza kuti wadzichepetsa pamaso panga, nkung'amba zovala zako numalira pamaso panga, Inenso ndamva pemphero lako, ndatero Ine Chauta. Tsono Ine ndidzakutenga, ukalondole makolo ako, ndipo udzaikidwa m'manda mwamtendere. Motero maso ako sadzaona zoipa zija zimene ndidzabweretsa pa mzinda uno ndi pa anthu ake.” Tsono anthu aja adabwerera nakanena mau amenewo kwa mfumu. Pamenepo mfumu idatumiza mau kukaitana akuluakulu onse a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti adzasonkhane. Ndipo mfumuyo idapita ku Nyumba ya Chauta, pamodzi ndi anthu onse a ku Yuda, nzika za mu Yerusalemu, ansembe ndi Alevi, ndiponso anthu onse aakulu ndi aang'ono omwe. Tsono iye adaŵerenga, pamaso pao, momveka ndithu, mau onse a m'buku lija lachipangano limene lidaapezeka m'Nyumba ya Chauta. Kenaka mfumu idaimirira pamalo pake, ndipo idachita chipangano pamaso pa Chauta kuti idzatsata njira za Chauta, ndipo kuti idzasunga mau, malamulo ndi malangizo ake ndi mtima wake wonse ndi moyo wake wonse, ndipo kuti idzagwiritsa ntchito mau a chipangano olembedwa m'bukulo. Tsono Yosiya adauza anthu onse amene anali mu Yerusalemu ndi ku Benjamini kuti azisunga chipanganocho. Ndipo nzika za mu Yerusalemu zidatsatadi chipangano cha Mulungu, Mulungu wa makolo ao. Kenaka Yosiya adachotsa zinthu zonyansa zonse ku maiko onse a Aisraele, nakakamiza anthu onse okhala ku Israele kuti azitumikira Chauta, Mulungu wao. Motero anthuwo sadaleke kutsata Chauta, Mulungu wa makolo ao, pa masiku onse a Yosiya. Yosiya adachita Paska ku Yerusalemu, kuchitira Chauta. Adapha mwanawankhosa wa Paska pa tsiku la 14 la mwezi woyamba. Adaika ansembe pa maudindo ao, namaŵalimbitsa mtima pa ntchito yotumikira ku Nyumba ya Chauta. Pambuyo pake adauza Alevi onse amene ankaphunzitsa Aisraele ndipo anali opatulikira Chauta, kuti, “Muike bokosi lopatulika m'Nyumba imene Solomoni mwana wa Davide, mfumu ya Israele, adamanga. Simuzidzalisenzanso pa mapewa anu ai. Mugaŵikane m'magulu malinga ndi mabanja anu, potsata zimene adalemba Davide mfumu ya Israele ndi zimene adalemba Solomoni mwana wake. Muziimirira ku malo opatulika potsata magulu a mabanja a abale anu amene sali ansembe. Ndipo banja lililonse la Alevi likhale ndi chigawo chake. Tsono muphe mwanawankhosa wa Paska, ndipo mudziyeretse. Muthandize abale anu, kuti zipherezere zimene Chauta adalankhula kudzera mwa Mose.” Tsono Yosiya adapereka kwa anthu wamba anaankhosa ndi anaambuzi okwanira 30,000 ndiponso ng'ombe zamphongo 3,000, zopereka za Paska. Zimenezi adazitenga pa chuma cha mfumu. Nduna zakenso zidapereka mwaufulu kwa anthu, kwa ansembe ndi kwa Alevi. Hilikiya, Zekariya ndi Yehiyele, atsogoleri a ku Nyumba ya Mulungu, adapereka kwa ansembe zopereka izi za Paska: anaankhosa ndi anaambuzi 2,600, ndiponso ng'ombe zamphongo 300. Konaniya nayenso, Semaya ndi Netanele, abale ake, pamodzi ndi Hasabiya, Yeiyele ndi Yozabadi, atsogoleri a Alevi, adapereka kwa Alevi zopereka izi za Paska: anaankhosa ndi anaambuzi 5,000, ndiponso ng'ombe zamphongo 500. Zonse zidayenda bwino malinga ndi mwambo wake: ansembe adakaima ku malo ao ndipo Alevi adakakhala m'magulu mwao, potsata ulamuliro wa mfumu. Ndipo adapha mwanawankhosa wa Paska. Tsono ansembe adawaza magazi amene adaŵalandira kwa Alevi, pamenepo nkuti Aleviwo akusenda nyamazo. Adapatula nsembe zopsereza, kuti azipereke potsata magulu a mabanja a anthu wamba, pamene ankapereka zao kwa Chauta, monga momwe zidaalembedwera m'buku la Mose. Ndipo adachitanso chimodzimodzi ndi ng'ombe zija. Tsono adaotcha mwanawankhosa wa Paska pa moto, potsata mwambo. Adaphika nyama yamwanawankhosa ya Paska m'mbiya, m'mitsuko ndi m'ziwaya. Ndipo adazipereka mofulumira kwa anthu osakhala ansembe. Pambuyo pake ankakonza zao ndi za ansembe, chifukwa chakuti ansembe, ana a Aaroni, anali otanganidwa ndi kupereka nsembe zopsereza ndi kutentha mafuta mpaka usiku. Choncho Alevi ankakonza zao ndiponso za ansembe, ana a Aaroni. Anthu oimba nyimbo, ana a Asafu, anali atakhala m'malo mwao potsata lamulo la Davide, la Asafu, la Hemani ndi la Yedutuni, mneneri wa mfumu. Alonda apazipata anali ku chipata chilichonse. Choncho kunali kosafunika kuti achokepo pa ntchito yao, poti abale ao Alevi ankaŵakonzera zonse. Motero ntchito zonse za Chauta zidakonzeka tsiku limenelo, kuti anthu achite Paska ndi kupereka nsembe zopsereza pa guwa la Chauta, potsata lamulo la mfumu Yosiya. Choncho Aisraele amene anali pamenepo adachita Paska nthaŵi imeneyo, ndipo pa masiku asanu ndi aŵiri adachita chikondwerero cha buledi wosafufumitsa. Sidachitikepo Paska yofanafana ndi imeneyi ku Israele chiyambire nthaŵi ya Samuele, mneneri uja. Panalibe ndi imodzi yomwe mwa mafumu a Aisraele imene idachitapo Paska monga imene adachita Yosiya, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi, Ayuda ndi Aisraele onse amene analipo, kudzanso nzika za mu Yerusalemu. Adachita Paska imeneyi pa chaka cha 18 cha ufumu wa Yosiya. Zitapita zimenezi ndipo Yosiya atakonza Nyumba ya Chauta, Neko, mfumu ya ku Ejipito, adapita kukamenya nkhondo ku Karikemisi ku mtsinje wa Yufurate, ndipo Yosiya adapita kukamenyana naye. Koma Neko adatuma amithenga kwa iyeyo kukamufunsa kuti, “Kodi iwe mfumu ya ku Yuda, ukuti tichitane chiyani? Ine sindibwera kudzalimbana ndi iwe lero, koma ndidzalimbana ndi banja limene ndikumenyana nalo nkhondo. Ndipo Mulungu wandilamula kuti ndifulumire. Siya kukangana ndi Mulungu amene ali nane, kuwopa kuti angakuwononge.” Koma Yosiya sadachoke ndipo adadzizimbaitsa kuti amenyane naye nkhondo. Sadasamale mau a Nekoyo amene Mulungu adaalankhula, koma adakamenyana ku chigwa cha Megido. Ndipo anthu oponya mivi adamlasa mfumu Yosiya. Apo mfumuyo idauza anyamata ake kuti, “Chotseni, poti ndalasidwa koipa.” Anyamata akewo adamchotsa pa galetalo namkweza pa galeta lake lachiŵiri, napita naye ku Yerusalemu. Ndipo adafa, naikidwa m'manda a makolo ake. Anthu onse a ku Yuda ndi a mu Yerusalemu adamulira Yosiya. Yeremiya nayenso adapeka nyimbo yamaliro chifukwa cha Yosiyayo. Anthu onse oimba nyimbo, amuna ndi akazi omwe, akhala akunena za Yosiya pomlira mpaka lero lino. Zimenezi zakhala ngati mwambo ku Israele, ndipo zidalembedwa m'buku lotchedwa “Madandaulo.” Tsono ntchito zina zonse za Yosiya ndi ntchito zake zabwino zimene adazichita, potsata zimene zidalembedwa m'malamulo a Chauta, ntchito zake zoyamba ndi zomalizira, zonsezo zidalembedwa m'buku la mafumu a ku Israele ndi a ku Yuda. Anthu am'dzikomo adatenga Yehowahazi mwana wa Yosiya, namlonga ufumu m'malo mwa atate ake ku Yerusalemu. Yehowahazi anali wa zaka 23 pamene ankaloŵa ufumu. Ndipo adalamulira miyezi itatu ku Yerusalemu. Pambuyo pake mfumu ya ku Ejipito idamchotsa Yehowahaziyo ku Yerusalemu, ndipo idakhometsa dziko msonkho wokwanira makilogramu 3,400 a siliva ndi 34 a golide. Tsono mfumu ya ku Ejipito idakhazika Eliyakimu, mbale wake wa Yehowahazi, kuti akhale mfumu yolamulira ku Yuda ndi ku Yerusalemu. Ndipo adasintha dzina lake kuti akhale Yehoyakimu. Koma Yehowahazi uja Neko adamtenga kupita naye ku Ejipito. Yehoyakimu anali wa zaka 25 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka khumi ndi chimodzi ku Yerusalemu. Iyeyo ankachita zoipa pamaso pa Chauta, Mulungu wake. Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, adabwera kudzamenyana naye nkhondo. Adammanga maunyolo kunka naye ku Babiloni. Nebukadinezara adatenganso ziŵiya za ku Nyumba ya Mulungu kunka nazo ku Babiloni. Ndipo adakaziika ku nyumba yake yaufumu ku Babiloniko. Tsono ntchito zina zonse za Yehoyakimu ndi zoipa zimene ankachita zidalembedwa m'buku la mafumu a ku Israele ndi a ku Yuda. Ndipo Yehoyakini mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake. Yehoyakini anali wa zaka 18 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira miyezi itatu ndi masiku khumi ku Yerusalemu. Iyeyo ankachita zoipa pamaso pa Chauta. Pomatha chaka, mfumu Nebukadinezara adatuma anthu kukamtenga, ndipo adabwera naye ku Babiloni, pamodzi ndi ziŵiya zamtengowapatali za ku Nyumba ya Chauta. Tsono adakhazika Zedekiya mbale wake kuti akhale mfumu ya ku Yuda ndi Yerusalemu. Zedekiya anali wa zaka 21 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka khumi ndi chimodzi ku Yerusalemu. Ankachita zoipa pamaso pa Chauta, Mulungu wake. Iyeyo sadadzichepetse pamaso pa mneneri Yeremiya, amene ankalankhula mau ochoka m'kamwa mwa Chauta. Adapandukiranso mfumu Nebukadinezara amene anali atamlumbiritsa kwa Mulungu kuti adzamumvera. Koma Zedekiyayo adangoti nkhongo gwa, nkuumitsanso mtima wake, kuti asabwerere kwa Chauta, Mulungu wa Israele. Atsogoleri onse a ansembe, pamodzi ndi anthu omwe, adachita zosakhulupirika zambirimbiri potsata zoipa za mitundu ina ya anthu. Adaipitsa Nyumba ya Chauta imene Chautayo anali ataipatula kuti ikhale yake ku Yerusalemu. Chauta, Mulungu wa makolo ao, ankaŵatumira amithenga kaŵirikaŵiri, chifukwa chakuti ankaŵamvera chifundo anthu ake ndi malo ake amene Iye ankakhala. Koma anthuwo ankapeputsabe amithengawo, namanyoza mau a Mulungu. Ndipo ankaŵaseka aneneri ake, mpaka Chauta adakwiyira anthu ake, ndipo panalibenso mankhwala ochiritsa. Nchifukwa chake adaŵautsira mfumu ya Ababiloni. Iwowo adapha anyamata ao ndi lupanga ku Nyumba ya Chauta wao. Ndipo sadachitire chifundo anyamata kapena anamwali, ndoda kapena nkhalamba. Chauta adaŵapereka onsewo kwa mfumu ya Ababiloni. Adaperekanso ziŵiya zonse za ku Nyumba ya Chauta, zazikulu nzazing'ono zomwe, pamodzi ndi chuma chonse cha ku Nyumba ya Mulungu ndiponso chuma cha ku nyumba ya mfumu, pamodzi ndi chuma cha nduna zake. Zonsezo adapita nazo ku Babiloni. Kenaka adatentha Nyumba ya Chauta, nagwetsa linga lonse la Yerusalemu. Adatenthanso nyumba zonse zaufumu, naononga ziŵiya zonse zamtengowapatali. Anthu amene adapulumuka ku lupanga, adaŵatenga ukapolo kupita nawo ku Babiloni. Kumeneko adasanduka anthu oitumikira mfumuyo ndi ana ake, mpaka ufumu wa Persiya utakhazikitsidwa, kuti zipherezere zimene Chauta adaalankhula kudzera mwa Yeremiya, zakuti, “Dzikoli lidzakhala lopasuka kwa zaka 70, kuti masabata opuma amene sanachitike, akwaniritsidwe.” Tsono chaka choyamba cha ufumu wa Kirusi, mfumu ya ku Persiya, Chauta adautsa mtima wa Kirusiyo, kuti alengeze ku maiko onse a ufumu wake mpaka kulemba kumene. Adachita choncho kuti zimene Chauta adaalankhula kudzera mwa Yeremiya zipherezere. Adati, “Kirusi, mfumu ya ku Persiya, akunena kuti, ‘Chauta, Mulungu wakumwamba, wandipatsa ine maufumu onse pa dziko lapansi. Ndipo wandilamula kuti ndimmangire Nyumba ku Yerusalemu, ku Yuda. Aliyense mwa inu nonse amene ali munthu wa Chauta, Chauta Mulungu wakeyo akhale naye. Ndipo apite.’ ” Chaka choyamba cha ulamuliro wa Kirusi, mfumu ya ku Persiya, Chauta adachitadi zimene adaanena kudzera mwa Yeremiya. Adaika maganizo mumtima mwa Kirusi, ndipo iye adalengeza m'dziko lake lonse ndi mau apakamwa, mpakanso ochita kulemba. Adati, “Kirusi, mfumu ya ku Persiya, akunena kuti, ‘Chauta, Mulungu Wakumwamba, wandipatsa ine maiko onse a pa dziko lonse lapansi, ndipo wandilamula kuti ndimmangire Nyumba ku Yerusalemu, ku dziko la Yuda. Tsono inu nonse amene muli akeake, Mulungu wanuyo akhale nanu. Aliyense mwa inu apite ku Yerusalemu, ku dziko la Yuda, kuti akamange Nyumba ya Chauta, Mulungu wa Israele. Iyeyo ndiye Mulungu amene amampembedza ku Yerusalemu. Motero kulikonse kumene anthu otsalawo amakhala, athandizidwe ndi eni dzikolo. Aŵapatse siliva ndi golide, katundu ndi ziŵeto, ndi zopereka zaufulu zoti akapereke ku Nyumba ya Mulungu, imene ili ku Yerusalemu.’ ” Choncho atsogoleri amabanja a fuko la Yuda ndi la Benjamini, ndiponso ansembe ndi Alevi, adayamba kukonzeka, aliyense amene mumtima mwake Mulungu adamupatsa maganizo oti apite kukamanganso Nyumba ya Chauta ku Yerusalemu. Onse oyandikana nawo adaŵathandiza poŵapatsa ziŵiya zasiliva, golide, katundu, ziŵeto ndiponso mphatso zamtengowapatali, kuphatikizapo zopereka zija zimene ankazipereka mwaufulu. Nayenso mfumu Kirusi adatulutsa ziŵiya za ku Nyumba ya Chauta zimene Nebukadinezara adaazitenga kuzichotsa ku Yerusalemu, kudzaziika m'nyumba ya milungu yake. Kirusi, mfumu ya ku Persiya, idazitulutsa zimenezi nkuzipereka kwa Metiredati, msungachuma wake, amene adaziŵerenga pamaso pa Sesibazara, nduna yaikulu ya ku dziko la Yuda. Chiŵerengero chake chinali chotere: Mabeseni agolide 30 a zopereka, mabeseni asiliva 1,000 a zopereka, zofukizira 29, timikhate tagolide 30, timikhate tasiliva 2,410, ndi ziŵiya zinanso 1,000. Ziŵiya zagolide ndi zasiliva zonse pamodzi zidakwanira 5,400. Zonsezi ndizo zimene Sesibazara adabwera nazo pamene akuukapolo aja ankabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku Babiloni. Naŵa anthu a m'chigawo cha Yuda amene adabwerako ku ukapolo, omwe Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, adaaŵagwira nkupita nawo ku ukapolo ku Babiloni. Anthuwo adabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wa makolo ake. Adabwera pamodzi ndi atsogoleri aŵa: Zerubabele, Yesuwa, Nehemiya, Seraya, Reelaya, Mordekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu ndi Baana. Nachi chiŵerengero cha anthu aamuna a Aisraele: A banja la Parosi, 2,172. A banja la Sefatiya, 372. A banja la Ara, 775. A banja la Pahatimowabu, ndiye kuti zidzukulu za Yesuwa ndi Yowabu, 2,812. A banja la Elamu, 1,254. A banja la Zatu, 945. A banja la Zakai, 760. A banja la Bani, 642. A banja la Bebai, 623. A banja la Azigadi, 1,222. A banja la Adonikamu, 666. A banja la Bigivai, 2,056. A banja la Adini, 454. A banja la Atere, ndiye kuti la Hezekiya, 98. A banja la Bezai, 323. A banja la Yora, 112. A banja la Hasumu, 223. A banja la Gibara, 95. Amuna a ku Betelehemu, 123. Amuna a ku Netofa, 56. Amuna a ku Anatoti, 128. A banja la Azimaveti, 42. A banja la Kiriyati-Arimu, Kefira ndi Beeroti, 743. A banja la Rama ndi Geba, 621. Amuna a ku Mikimasi, 122. Amuna a ku Betele ndi ku Ai, 223. A banja la Nebo, 42. A banja la Magabisi, 156. A banja la Elamu wina, 1,254. A banja la Harimu, 320. A banja la Lodi, Hadidi ndi Ono, 725. A banja la Yeriko, 345. A banja la Sena, 3,630. Ansembe anali aŵa: a banja la Yedaya, ndiye kuti zidzukulu za Yesuwa, 973. A banja la Imeri, 1,052. A banja la Pasuri, 1,247. A banja la Harimu, 1,017. Alevi anali aŵa: a banja la Yesuwa ndi la Kadimiyele, ndiye kuti zidzukulu za Hodaviya, 74. Oimba nyimbo anali aŵa: a banja la Asafu, 128. Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali aŵa: a banja la Salumu, a banja la Atere, a banja la Talimoni, a banja la Akibu, a banja la Hatita, ndi a banja la Sobai, onse pamodzi 139. Antchito a ku Nyumba ya Mulungu anali aŵa: a banja la Ziha, a banja la Hasufa, a banja la Tabaoti, a banja la Kerosi, a banja la Siyaha, a banja la Padoni, a banja la Lebana, a banja la Hagaba, a banja la Akubu, a banja la Hagabu, a banja la Salimai, a banja la Hanani, a banja la Gidele, a banja la Gahara, a banja la Reaya, a banja la Rezini, a banja la Nekoda, a banja la Gazamu, a banja la Uza, a banja la Paseya, a banja la Bosai, a banja la Asina, a banja la Meunimu, a banja la Nefisimu, a banja la Bakibuki, a banja la Hakufa, a banja la Harihuri, a banja la Baziluti, a banja la Mehida, a banja la Harisa, a banja la Barikosi, a banja la Sisera, a banja la Tema, a banja la Neziya ndi a banja la Hatifa. Mabanja a antchito ake a Solomoni anali aŵa: a banja la Sotai, a banja la Hasopereti, a banja la Peruda, a banja la Yaala, a banja la Darikoni, a banja la Gidele, a banja la Sefatiya, a banja la Hatili, a banja la Pokereti-Hazebaimu ndi a banja la Ami. Antchito onse a ku Nyumba ya Mulungu, kuphatikizapo zidzukulu za antchito a Solomoni, onse analipo 392 pamodzi. Anthu ali m'munsiŵa ndiwo amene adabwera kuchokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adani ndi ku Imeri, ngakhale sankatha kutsimikiza kuti makolo ao kapena mafuko ao analidi Aisraele enieni kapena ai. A banja la Delaya, a banja la Tobiya ndi a banja la Nekoda, 642. Ndiponso ena mwa ansembe anali aŵa: a banja la Habaya, a banja la Hakozi ndi a banja la Barizilai (kunena amene adaakwatira mmodzi mwa ana aakazi a Barizilai Mgiliyadi, nkutenga dzina la bambo waoyo). Iwoŵa adafunafuna maina ao m'buku lolongosola kaundula wa mafuko ao, koma maina ao sadapezekemo. Choncho adaŵachotsa pa unsembe, naŵaŵerenga kuti ngodetsedwa pa chipembedzo. Bwanamkubwa adaŵauza anthuwo kuti asamadye nawo chakudya choperekedwa kwa Mulungu, mpaka wansembe wodziŵa kuwombeza ndi Urimu ndi Tumimu atapezeka. Chiŵerengero cha anthu onse obwerako ku ukapolo aja chinali 42,360. Kuwonjezera pamenepo, panalinso antchito ao aamuna ndi aakazi okwanira 7,337. Anali nawonso anthu oimba nyimbo, amuna ndi akazi omwe, okwanira 200. Akavalo ao analipo 736, nyulu zao zinalipo 245, ngamira zao zinalipo 435 ndipo abulu ao analipo 6,720. Pamene adabwera ku Nyumba ya Chauta ku Yerusalemu, atsogoleri ena a mabanja adapereka mphatso zaufulu, kuperekera Nyumba ya Mulungu, kuti imangidwenso pamalo pake pakale. Adapereka kwa msungachuma wa ntchitoyo molingana ndi chuma chao, golide wa makilogaramu 500, ndi siliva wa makilogaramu 2,800, ndiponso zovala za ansembe zokwanira 100. Ansembe, Alevi ndi anthu ena ankakhala mu mzinda wa Yerusalemu ndi m'midzi yake yozungulira. Anthu oimba nyimbo, alonda ndi antchito a ku Nyumba ya Mulungu, ndiponso Aisraele ena onse, ankakhala m'midzi ya makolo ao. Pa mwezi wachisanu ndi chiŵiri, ana a Aisraele ali m'midzi mwao, anthu adasonkhana ku Yerusalemu ndi cholinga chimodzi. Pamenepo Yesuwa, mwana wa Zadoki, ndi ansembe anzake, pamodzi ndi Zerubabele, mwana wa Sealatiele, ndi abale ake, adayamba kumanga guwa la Mulungu wa Aisraele. Adafuna kuti aziperekapo nsembe zopsereza, monga adalembera m'buku la malamulo a Mose, munthu wa Mulungu uja. Ngakhale kuti ankaopa mitundu ina ya anthu am'maikowo, adamanga guwalo pa maziko ake akale, ndipo ankapereka nsembe zopsereza kwa Chauta paguwapo m'maŵa ndi madzulo. Ankasunga tsiku la chikondwerero cha misasa monga momwe kudalembedwera. Masiku onse ankaperekanso nsembe zopsereza potsata chiŵerengero chake chofunika tsiku ndi tsiku, monga kudalembedwera. Pambuyo pake ankapereka nsembe zopsereza monga mwa nthaŵi zonse, nsembe zopereka pokhala mwezi ndi pa masiku onse achikondwerero oikidwa otamandira Chauta, kudzanso nsembe zaufulu zopereka kwa Chauta. Kuyambira pa tsiku loyamba la mwezi wachisanunchiŵiri, adayamba kupereka nsembe zopserezazi kwa Chauta. Koma maziko a Nyumba ya Mulungu anali asanamangidwebe. Tsono anthu adapereka ndalama kwa amisiri osema miyala ndi kwa amisiri a matabwa. Adatumiza chakudya, zakumwa ndi mafuta kwa anthu a ku Sidoni ndi ku Tiro, kuti azigulira mitengo ya mkungudza ya ku Lebanoni. Mitengoyo adafika nayo ku nyanja mpaka ku mzinda wa Yopa. Zonsezi ankazichita potsata chilolezo cha Kirusi, mfumu ya ku Persiya. Tsono chaka chachiŵiri atabwera ku Yerusalemu, ku mabwinja kumene kunali Nyumba ya Mulungu yakale, mwezi wachiŵiri, Zerubabele mwana wa Sealatiele ndiponso Yesuwa mwana wa Yozadaki, adayambapo ntchito pamodzi ndi abale ao otsala, ansembe ndi Alevi, ndi onse amene anali atabwera ku Yerusalemu kuchokera ku ukapolo. Adasankha Alevi kuyambira anthu a zaka makumi aŵiri zakubadwa ndi opitirirapo, kuti aziyang'anira ntchito yomanga Nyumba ya Chauta. Yesuwa ndi ana ake kudzanso achibale ake, ndiponso Kadimiyele ndi ana ake, ana a Yuda, onsewo pamodzi adasenza udindo woyang'anira anthu antchito ku Nyumba ya Mulungu, kuphatikizapo ana a Henadadi, ndiponso Alevi ndi ana ao ndi achibale ao. Tsono amisiri omanga nyumba atamanga maziko a Nyumba ya Chauta, ansembe adadza akuimba malipenga atavala zovala zaunsembe. Ndipo Alevi, zidzukulu za Asafu, adadza akuimba ziwaya zamalipenga ndi kutamanda Chauta, potsata malangizo a Davide mfumu ya Aisraele. Ankaimba ndi mavume mopolokezana, motamanda ndi mothokoza Chauta. Ankati, “Chauta ndi wabwino, chikondi chake pa Israele nchamuyaya.” Ndipo anthu onse ankafuula kwambiri pamene ankatamanda Chauta chifukwa choti maziko a Nyumba ya Chauta anali akumangidwa. Koma ambiri mwa ansembe, Alevi ndi atsogoleri a mabanja, ndiponso nkhalamba zimene zidaaona nyumba yoyamba, adalira mokweza mau, ataona maziko a nyumba imeneyi akumangidwa. Komabe ambirinso ankafuula mokondwa. Choncho anthu sankatha kusiyanitsa liwu lofuula mokondwerera ndi liwu la anthu olira, popeza kuti anthuwo ankafuula kwambiri ndipo liwu la kufuulako linkamveka kutali. Adani a Yuda ndi a Benjamini adaamva kuti anthu obwerako ku ukapolo aja akumangira Nyumba Chauta, Mulungu wa Aisraele. Ndiye adadza kwa Zerubabele ndi kwa atsogoleri a mabanja, naŵauza kuti, “Mutilole kuti timange nawo, pakuti ife timapembedza Mulungu wanu monga momwe mumachitira inu, ndipo takhala tikupereka nsembe kwa Iye kuyambira nthaŵi ya Ezaradoni, mfumu ya ku Asiriya, amene adatifikitsa kuno.” Koma Zerubabele, Yesuwa, ndi atsogoleri ena otsala a mabanja a m'dziko la Israele adaŵayankha kuti, “Sitikusoŵa chithandizo chanu pa ntchito iyi yomangira Nyumba Mulungu wathu. Koma ife tokha tidzammangira Nyumba Chauta, Mulungu wa Israele, monga mfumu Kirusi, mfumu ya ku Persiya, adatilamula.” Atamva zimenezi anthu a m'dzikomo adayamba kutayitsa mtima Ayuda, ndi kuŵachititsa mantha kuti aleke ntchito yomangayo. Adalemba akuluakulu ena kuti alepheretse cholinga chao cha pa ntchitoyo pa nthaŵi yonse ya Kirusi, mfumu ya ku Persiya, ngakhalenso mpaka pamene Dariusi, mfumu ya ku Persiya ankalamulira dzikolo. Pamene mfumu Ahasuwero adayamba kulamulira dziko, adani aja adalemba kalata yoneneza nzika zija za ku Yuda ndi za ku Yerusalemu. Chimodzimodzinso pa nthaŵi ya Arita-kisereksesi, mfumu ya ku Persiya, Bisilamu, Mitiredati, Tabiyele ndi anzao ena, adalemba inanso kalata kwa Arita-kisereksesiyo. Kalatayo adailemba m'Chiaramu, ndipo poiŵerenga ankachita kutanthauzira. Kenaka Rehumu Bwanamkubwa ndi Simisai mlembi wake, nawonso adalemba yao kalata kwa mfumu Arita-kisereksesi yoneneza anthu a ku Yerusalemu. Adalemba motere: “Kalatayi ikuchokera kwa Rehumu bwanamkubwa, mlembi Simisai ndi anzao aŵa: aweruzi, nduna ndi akuluakulu ena, anthu a ku Persiya ndi ku Ereki, ku Babiloniya, ndi ku Susa, m'dziko la Elami. Enanso ndi mitundu ina imene Osinapara, wamkulu ndi womveka uja, adaisamutsa ndi kuikhazika m'mizinda ya Samariya ndi kwinanso m'madera a m'chigawo chimene chili Patsidya pa Yufurate.” Mau ake a m'kalata imene adatumizayo ndi aŵa: “Zikomo, amfumu Arita-kisereksesi, ife atumiki anu, a m'chigawo cha Patsidya pa Yufurate, poyamba tikukupatsani moni. Amfumu, tikuti mudziŵeko kuti Ayuda omwe adabwera kuno kuchokera kwanuko, apita ku Yerusalemu. Akumanganso mzinda wopanduka ndi woipa uja. Akumaliza makoma ake ndipo akukonza maziko. Tsonotu amfumu, mudziŵe kuti akaumanganso mzinda umenewu ndi kumaliza kumanga makoma ake, ndiye kuti anthu aja adzaleka kukhoma msonkho ndi kupereka kasitomo kapena msonkho wa kanthu kena kalikonse, ndipo chuma choloŵa m'thumba la mfumu chidzachepa. Tsono popeza kuti ife ndife akadyere kwa mfumu, si bwino kuti tizingopenya zinthu zochititsa mfumu manyazi. Nchifukwa chake tikutumiza mau kwa inu mfumu kuti mudziŵe zonse. Ndi bwino kuti pachitike kafukufuku m'buku la mbiri yakale ya makolo anu. M'buku lazakalemo mudzapeza ndi kuŵerengamo kuti mzinda umenewo ndi waupandu, wosautsa mafumu ndi nduna zam'madera zomwe. Kuyambira kale wakhala ukuchita zoukira ulamuliro uliwonse. Nchifukwa chake mzinda umene uja adausandutsa bwinja. Tikukudziŵitsani inu amfumu kuti ngati mzinda umenewu aumanganso ndi kutsirizanso makoma ake, ndiye kuti inuyo simudzatha kumalamulirabe m'chigawo cha Patsidya pa Yufuratecho.” Tsono mfumuyo idayankha kalatayo motere, “Bwanamkubwa Rehumu ndi mlembi Simisai, ndi anzanu ena amene akukhala ku Samariya ndi m'chigawo cha Patsidya pa Yufurate, ndikuti moni. Kalata imene mudatumiza, aiŵerenga pamaso panga momveka bwino. Ine nditalamula kuti afufuzefufuze nkhaniyi, kwapezekadi kuti mzinda umenewo udaaukira mafumu kale, ndipo kuti zaupandu ndi zoukira zinkachitikadi m'menemo. Mafumu amphamvu adakhala akulamulira Yerusalemu ndi chigawo chonsecho cha Patsidya pa Yufurate, namalandira kasitomo ndi msonkho pa kanthu kena kalikonse. Tsono inu mulembe lamulo loŵaletsa anthu amenewo kuti asamangenso mzinda umenewo, mpaka ine nditaloleza. Ndithu zimenezi musachedwetse. Nanga ndingalole bwanji kuti zoononga zotere zikule ndi kupweteka ine mfumu?” Kalata ya mfumu Arita-kisereksesiyo ataiŵerenga pamaso pa Rehumu ndi mlembi Simisai ndi anzao, iwowo adapita msangamsanga ku Yerusalemu, nakaŵaletsa Ayuda aja mwamphamvu kuti asapitirize ntchito yao. Motero ntchito yomanga Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu idalekeka mpaka chaka chachiŵiri cha ufumu wa Dariusi, mfumu ya ku Persiya. Nthaŵi imeneyo aneneri aŵa, Hagai ndi Zekariya mwana wa Ido, adayamba kulankhula kwa Ayuda okhala m'dziko la Yuda ndi mu Yerusalemu. Ankalankhula m'dzina la Mulungu wa Israele amene anali nawo. Atamva mauwo, Zerubabele mwana wa Sealatiele ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki adanyamuka nakayambanso kumanga Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Aneneri a Mulunguwo nawonso anali nawo pamodzi namaŵathandiza. Nthaŵi yomweyo Tatenai, bwanamkubwa wa chigawo cha Patsidya pa Yufurate ndi Setari-Bozenai, pamodzi ndi anzao adapita kwa iwowo, ndipo adalankhula nawo naŵafunsa kuti, “Adakulamulani ndani kuti mumange Nyumba imeneyi ndi kumaliza khoma lake?” Adaŵafunsanso kuti, “Kodi anthu amene akumanga Nyumba imeneyiŵa, maina ao ndani?” Koma Mulungu wao ankaŵasamalira atsogoleri a Ayuda, ndipo choncho anthu aja adaganiza zoti asaŵaletse Ayudawo kumanga mpaka atalembera mfumu Dariusi kalata, nkulandiranso yankho lake pa nkhani imeneyi. Nayi kalata yomwe Tatenai, bwanamkubwa wa dera la Patsidya pa Yufurate, ndiponso Setari-Bozenai ndi anzake, akazembe omwe anali m'chigawo cha Patsidya pa Yufurate, adatumiza kwa mfumu Dariusi. Adalemba kuti, “Kwa mfumu Dariusi, ulamuliro wanu ukhale ndi mtendere wonse. Inu mfumu, mudziŵe kuti ife tidaapita ku dziko la Yuda ku Nyumba ya Mulungu wamkulu. Nyumbayo ikumangidwa ndi miyala ikuluikulu, ndipo akuyalika mitengo pa makoma. Ntchito imeneyi ikuchitika mwachangu, ndipo ikuyenda bwino kwambiri poigwira anthuwo. Tsono tidaŵafunsa atsogoleriwo kuti, ‘Kodi adakulamulani ndani kuti mumange Nyumba imeneyi ndi kutsiriza makoma ake?’ Tidaŵafunsanso maina ao, kuti tikalemba maina a atsogoleri ao, tidzakudziŵitseni. Anthuwo adatiyankha kuti, ‘Ife ndife atumiki a Mulungu wa dziko lakumwamba ndi wa dziko lapansi, ndipo tikumanganso Nyumba imene mfumu ina yamphamvu ya Israele idaamanga ndi kuimaliza zaka zamakedzana. Koma chifukwa choti makolo athu adaakwiyitsa Mulungu Wakumwamba, Iye adaaŵapereka kwa Nebukadinezara, Mkaldea, mfumu ya ku Babiloni. Ndiye amene adaaononga nyumba ino, natenga anthu onse kunka nawo ku ukapolo ku Babiloni. Komabe chaka choyamba cha ufumu wa Kirusi mfumu ya ku Babiloni, Kirusiyo adapanga lamulo lakuti Nyumba ya Mulunguyi imangidwenso. Ndipo ziŵiya zagolide ndi zasiliva za ku Nyumba ya Mulungu zimene Nebukadinezara adaatulutsa ku Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu ndi kukazilonga m'nyumba ya milungu ya ku Babiloni, zomwezonso mfumu Kirusiyo adazitulutsa ku nyumba ya milungu ya ku Babiloniyo, nazitumiza kwa munthu wina dzina lake Sesibazara, amene mfumu idampatsa ulamuliro mu Yerusalemu. Tsono mfumuyo idamuuza kuti, “Tenga ziŵiyazi, ukaziike m'Nyumba ya Mulungu ya ku Yerusalemu, ndipo Nyumbayo imangidwenso pa maziko ake akale.” Tsono Sesibazarayo adabwera, nayamba kumanga maziko a Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Kuyambira nthaŵi imeneyo mpaka tsopano yakhala ikumangidwa, ndipo siinathebe.’ Nchifukwa chake tsono, chikakukomerani inu mfumu, pachitike kafukufuku m'nyumba mosungira chuma ndi mabuku okhudza mbiri zakale ku Babiloniko, kuti tiwone ngati mfumu Kirusi adaaperekadi lamulo lonena za kumanganso Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Kenaka chonde, inu amfumu, mutidziŵitse zomwe zikukondwetseni kuti mugamule pa nkhani imeneyi.” Atalandira mauwo mfumu Dariusi adapanga lamulo ndipo kafukufuku adachitikadi ku Babiloni m'nyumba mosungira chuma ndi mabuku okhudza mbiri zakale. Tsono ku Ekibatana, likulu la dziko la Mediya, kudapezeka mpukutu m'mene mudaalembedwa kuti, “Chikumbutso.” Mau ake anali aŵa: “Pa chaka choyamba cha ufumu wake, mfumu Kirusi adapereka lamulo lalikulu lonena za Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Adalamula kuti Nyumbayo imangidwenso, ngati malo otsirirako nsembe. Maziko ake ayalidwe mwamphamvu pomwe paja pali maziko ake akale. Muutali mwake idzakhale mamita 27, muufupi mwake idzakhalenso mamita 27. Mudzamange mizere itatu ya miyala yaikulu ndi mzere umodzi wa matabwa. Ndalama zake zolipirira ntchitoyo zichokere m'thumba lachifumu. Tsono ziŵiya zagolide ndi zasiliva za ku Nyumba ya Mulungu zimene Nebukadinezara adaazitulutsa ku Yerusalemu kunka nazo ku Babiloni, zonsezo zibwezedwe, zipite ku Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Chilichonse chikabwezedwe pamalo pake m'Nyumba ya Mulunguyo.” Tsono mfumu Dariusi adayankha motere: “Inu Tatenai, bwanamkubwa wa dera la Patsidya pa Yufurate, ndiponso Setari-Bozenai pamodzi ndi anzanu, muchokeko kumeneko. Ntchito iyi yomanga Nyumba ya Mulungu muileke. Mlekeni bwanamkubwa wa ku dera la Yuda ndiponso atsogoleri akumeneko kuti amangenso Nyumba ya Mulunguyo pamalo pake ndithu. Kuwonjezera pamenepo, ndikupanga lamulo lonena za m'mene mudzaŵachitire atsogoleri a Ayudawo zothandiza pomanganso Nyumbayo. Anthuwo muŵalipire msanga kuchokera m'thumba lachifumu, kuchotsa pa msonkho wa dera la Patsidya pa Yufurate. Ndipo zonse zofunikira, monga anaang'ombe, nkhosa zamphongo kapena anaankhosa, zoperekera nsembe zopsereza kwa Mulungu Wakumwamba, kapena tirigu, mchere, vinyo ndi mafuta, monga m'mene ansembe a ku Yerusalemu angafunire, muziŵapatsa zimenezo tsiku ndi tsiku osalephera. Zimenezi zichitike kuti azipereka nsembe za fungo lokomera Mulungu Wakumwamba, ndi kuti anthuwo apempherere moyo wa mfumu ndi wa ana ake. Ndikupanganso lamulo lakuti ngati wina aliyense asintha zimene ndalamulazi, ndiye kuti adzasololako mtanda wa nyumba yake nadzamkhomera pamenepo, ndipo nyumba yakeyo adzaisandutsa dzala. Mulungu amene adasankhula Yerusalemu kuti akhale malo ompembedzerako, achotse mfumu iliyonse kapena anthu amene adzayerekeze kusintha zimenezi kapena kuwononga Nyumba ya Mulungu yakumeneko. Ine Dariusi ndikuika lamuloli, aliyense alitsate mosamala kwambiri.” Tsono potsata mau amene mfumu Dariusi adaalamula, Tatenai, bwanamkubwa wa dera la Patsidya pa Yufurate, Setari-Bozenai ndi anzao adachita mosamala kwambiri zimene mfumu Dariusi adaalamula. Ndipo akulu a Ayuda adapititsa m'tsogolo ntchito yomanga ija. Iwo ankalimbikitsidwa ndi aneneri aja Hagai ndi Zekariya mwana wa Ido. Adamaliza ntchito yao yomanga Nyumba, monga momwe Mulungu wa Israele adaalamulira, ndiponso potsata lamulo la Kirusi, la Dariusi, ndi la Arita-kisereksesi, mafumu a ku Persiya. Nyumbayo adaimaliza kumanga pa tsiku lachitatu la mwezi wa Adara, chaka chachisanu ndi chimodzi cha ulamuliro wa mfumu Dariusi. Tsono Aisraele, ndiye kuti ansembe, Alevi ndi anthu ena onse amene anali atabwerako ku ukapolo, adachita chikondwerero cha kupereka Nyumba ya Mulungu mwachimwemwe. Pochita mwambo umenewo, anthuwo adapereka nsembe za ng'ombe zamphongo 100, nkhosa zamphongo 200, anaankhosa 400. Adaperekanso atonde khumi ndi aŵiri ngati nsembe yopepesera uchimo wa anthu onse, potsata chiŵerengero cha mafuko a Aisraele. Choncho adaŵakhazika ansembe ndi Alevi pa ntchito zao zotumikira Mulungu ku Yerusalemu, monga momwe zidalembedwera m'buku la Mose. Pa tsiku la 14 la mwezi woyamba, obwerako ku ukapolo aja adachita Paska. Ansembe ndi Alevi anali atadziyeretsa, tsono onsewo anali oyeradi. Choncho adapha mwanawankhosa wa Paska, kuphera onse amene adatuluka ku ukapolo, ansembe anzao ndi eniakewo. Nkhosa ya Paskayo adaidya Aisraele onse amene adatuluka ku ukapolo. Adadyakonso wina aliyense amene adaphatikana nawo, atadziyeretsa ku zonyansa za mitundu ina ya anthu akunja am'dzikomo, kuti apembedze Chauta, Mulungu wa Israele. Motero pa masiku asanu ndi aŵiri adasangalala pa chikondwerero cha buledi wosatupitsa. Zidatero chifukwa Chauta adaŵakondweretsa, ndipo adaatembenuza mtima wa mfumu ya ku Asiriya, kotero kuti idaŵakomera mtima niŵathandiza pa ntchito yomanga Nyumba ya Mulungu, Mulungu wake wa Aisraele. Zitapita zaka zambiri, pamene Arita-kisereksesi anali mfumu ya ku Persiya, panali wansembe wina dzina lake Ezara. Iyeyu anali mdzukulu wa Aaroni, mkulu wa ansembe woyamba wa Israele. Makolo ake anali aŵa: Seraya, mwana wa Azariya, mwana wa Hilikiya, mwana wa Salumu, mwana wa Zadoki, mwana wa Ahitubi, mwana wa Amariya, mwana wa Azariya, mwana wa Meraiyoti, mwana wa Zerahiya, mwana wa Uzi, mwana wa Buki, mwana wa Abisuwa, mwana wa Finehasi, mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni mkulu wa ansembe uja. Ezarayu anali wophunzira kwambiri wa za Malamulo amene Chauta, Mulungu wa Israele, adaapereka kwa Mose. Popeza kuti Chauta, Mulungu wake, adaamdalitsa Ezarayo, mfumu Arita-kisereksesi ankamupatsa zonse zimene ankapempha. Tsono chaka chachisanu ndi chiŵiri cha ufumu wa Arita-kisereksesi, Ezarayo adanyamuka kuchokera ku Babiloni kunka ku Yerusalemu pamodzi ndi Aisraele ena, ndiye kuti ansembe ndi Alevi, oimba nyimbo, alonda ndiponso anthu ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu. Ezarayo adafika ku Yerusalemu pa mwezi wachisanu wa chaka chachisanu ndi chiŵiri cha mfumu. Adanyamuka ku Babiloni pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu, nafika ku Yerusalemu ndi chithandizo cha Mulungu wake. Pakuti Ezara adaaika mtima wake pa kuphunzira Malamulo a Chauta ndi kuŵatsata. Ankafunitsitsanso kuphunzitsa Aisraele malamulo ndi malangizo a Chauta. Nayi kalata imene mfumu Arita-kisereksesi adapatsa wansembe Ezara, mlembi uja wophunzira kwambiri malamulo ndi malangizo amene Chauta adaapatsa Aisraele: “Ndine, Arita-kisereksesi, mfumu ya mafumu, ndikulembera iwe Ezara, wansembe ndi mlembi wa malamulo a Mulungu Wakumwamba. Tsopano ndikupanga lamulo lakuti Mwisraele aliyense kapena ansembe ao, kapena Alevi okhala m'dziko mwanga, amene afuna kuti apite ku Yerusalemu mwaufulu, apite nawe. Pakuti ine mfumu pamodzi ndi aphungu anga asanu ndi aŵiri tikukutuma kuti ukafunsitse za dziko la Yuda ndi mzinda wa Yerusalemu, kuti ukaone m'mene anthu akutsatira malamulo amene Mulungu wako adaŵapereka kwa iwe. Utenge siliva ndi golide zimene ine mfumu ndi aphungu anga tapereka mwaufulu kwa Mulungu wa Aisraele, amene Nyumba yake ili ku Yerusalemu. Utengenso siliva ndi golide yense amene mumpeze m'dziko lonse la Babiloni, ndiponso zopereka zimene anthu ndi ansembe adzapereka mwaufulu, mosakakamiza, kuperekera Nyumba ya Mulungu wao ya ku Yerusalemu. Tsono ndi ndalama zimenezi, mudzagule mwachangu ng'ombe zamphongo, nkhosa zamphongo ndi anaankhosa, pamodzi ndi nsembe zake zaufa ndiponso nsembe zake zazakumwa. Mudzapereke zimenezi pa guwa la ku Nyumba ya Mulungu wanu ya ku Yerusalemu. Ndalama zotsala muzigwiritse ntchito monga momwe inuyo ndi abale anu mungafunire malinga nkufuna kwa Mulungu wanu. Ziŵiya zimene akupatsanizi kuti muzitumikira nazo m'Nyumba ya Mulungu wanu, mukazipereke kwa Mulungu ku Yerusalemu. Ndipo china chilichonse chimene chingafunikire m'Nyumba ya Mulungu wanu, chimene mudzapeze danga loperekera, ndalama zake zogulira zidzatuluke m'thumba la chuma cha mfumu. “Tsono ine, mfumu Arita-kisereksesi, ndikulamula onse osunga chuma m'dera la Patsidya pa Yufurate, kuti zonse zimene wansembe Ezara, wophunzira wa malamulo a Mulungu Wakumwamba, adzapemphe kwa inu, zichitike mwachangu. Ngakhale afunika makilogaramu 3,400 a siliva, makilogaramu 10,000 a tirigu, malitara 2,000 a vinyo, ndi malitara 2,000 a mafuta, ndiponso mchere wochuluka chotani, zonsezo muzipereke monga m'mene zingafunikire. Zonse zimene Mulungu Wakumwamba alamule, zichitike mwachangu ku Nyumba ya Mulungu Wakumwamba, kuwopa kuti mkwiyo wake ungayakire mfumu ndi dziko lake ndi ana ake. Tikukudziŵitsaninso kuti kudzakhala kosaloledwa kumkhometsa msonkho uliwonse wansembe aliyense, Mlevi aliyense, woimba aliyense, mlonda kapena wantchito aliyense wa ku Nyumba ya Mulungu. “Ndiye iwe Ezara, potsata nzeru zimene Mulungu wako adakupatsazi, usankhe oyendetsa zinthu ndi aweruzi oti azilamulira anthu onse okhala m'dera la Patsidya pa Yufurate, anthu ake otsata malamulo a Mulungu wako. Ndipo anthu osadziŵa malamulowo uzidzaŵaphunzitsa. Aliyense amene sadzamvera malamulo a Mulungu wako kapena malamulo a mfumu, alangidwe kolimba, kapena kuphedwa, kapena kuchotsedwa m'dzikolo, kapena kumlanda katundu wake, kapena kumponya m'ndende.” Ezara adati, “Atamandike Chauta, Mulungu wa makolo athu, amene adaika nzeru zotere mu mtima wa mfumu, kuti apereke ulemu ku Nyumba ya Mulungu ya ku Yerusalemu. Ndiye amenenso adaonetsa chikondi chake chosasinthika pa ine kuti mfumu ndi aphungu ake ndi atsogoleri ake amphamvu andikomere mtima. Ndidalimba mtima popeza kuti Chauta Mulungu wanga anali nane, choncho ndidasonkhanitsa atsogoleri ambiri a Aisraele kuti apite nane pamodzi.” Nawu mndandanda wa maina a atsogoleri a mabanja amene adabwera nane kuchokera ku Babiloni, pa nthaŵi ya ufumu wa Arita-kisereksesi: Geresomo, wa fuko la Finehasi. Daniele, wa fuko la Itamara. Hatusi, mwana wa Sekaniya, wa fuko la Davide. Zekariya, wa fuko la Parosi. Iyeyu adalembedwa pamodzi ndi anthu ena okwanira 150. Eliehoenai, mwana wa Zerahiya, wa fuko la Pahatimowabu. Pamodzi ndi iyeyo panali anthu 200. Sekaniya, mwana wa Yahaziele, wa fuko la Zatu. Pamodzi ndi iyeyo panali anthu 300. Ebedi, mwana wa Yonatani, wa fuko la Adini. Pamodzi ndi iyeyo panali anthu 50. Yesaya, mwana wa Ataliya, wa fuko la Elamu. Pamodzi ndi iyeyo panali anthu 70. Zebadiya, mwana wa Mikaele, wa fuko la Sefatiya. Pamodzi ndi iyeyo panali anthu 80. Obadiya, mwana wa Yehiyele, wa fuko la Yowabu. Pamodzi ndi iyeyo panali anthu 218. Selomiti, mwana wa Yosofiya, wa fuko la Bani. Pamodzi ndi iyeyo panali anthu 160. Zekariya, mwana wa Bebai, wa fuko la Bebai. Pamodzi ndi iyeyo panali anthu 28. Yohanani, mwana wa Hakatani, wa fuko la Azigadi. Pamodzi ndi iyeyo panali anthu 110. Atsogoleri a fuko la Adonikamu, anthu amene adabwera pambuyo pake, anali Elifeleti, Yeiyele ndi Semaya, ndipo pamodzi ndi iwowo panali anthu 60. Atsogoleri a fuko la Bigivai anali Utai ndi Zakuri, ndipo pamodzi ndi iwowo panali anthu 70. Anthu onsewo ndidaŵasonkhanitsa ku mtsinje umene umafika mpaka ku mudzi wa Ahava, ndipo kumeneko tidagona m'zithando masiku atatu. Pamene ndinkayang'ana anthu ndi ansembe, ndidapeza kuti ana a Levi palibe. Tsono ndidaitana atsogoleri aŵa, Eliyezere, Ariyele, Semaya, Elinatani, Yaribu, Elinatani, Natani, Zekariya ndi Mesulamu, pamodzi ndi aphunzitsi aŵiri, Yoyaribu ndi Elinatani. Ndipo ndidaŵatuma kwa Ido, mtsogoleri wa malo otchedwa Kasifiya. Ndidaŵauza zoti akanene kwa Ido ndi kwa abale ake, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu ku Kasifiyako, kuti atitumizire anthu odzatumikira ku Nyumba ya Mulungu wathu. Chifukwa cha kutikomera mtima Mulungu wathu, Ido adatitumizira munthu wanzeru, mwana wa fuko la Mahili, mwana wa Levi, mwana wa Israele, dzina lake Serebiya, pamodzi ndi ana ake aamuna ndi achibale ake, anthu 18 pamodzi. Adatitumiziranso Hasabiya ndi Yeshaiya wa fuko la Merari, kudzanso achibale ake ndiponso ana ao, anthu makumi aŵiri. Panalinso atumiki a ku Nyumba ya Mulungu okwanira 220, amene Davide ndi nduna zake adaaŵasankha kuti azitumikira Alevi. Anthu onseŵa adalembedwa potsata maina ao. Ku mtsinje wa Ahavako, ndidalengeza kuti anthu onse asale zakudya, adzichepetse pamaso pa Mulungu wathu ndi kumpempha kuti atitsogolere ife ndi ana athu, ndiponso kuti ateteze katundu wathu pa ulendo wathu. Ndinali ndi manyazi kupempha mfumu kuti itipatse gulu la asilikali, ena oyenda pansi ndi ena okwera pa akavalo, oti atiteteze kwa adani athu pa njira. Tinali titauza mfumuyo kuti, “Mulungu wathu amaŵadalitsa onse okhulupirira Iye, koma amaŵakwiyira amene salabadako za Iye.” Choncho tidasala zakudya ndi kupemphera kwa Mulungu wathu kuti atiteteze, ndipo Iye adamva kupempha kwathu. Tsono ndidasankha atsogoleri a ansembe khumi ndi aŵiri aŵa, Serebiya ndi Hasabiya, pamodzi ndi abale ao khumi. Ndipo ndidaŵayesera siliva ndi golide, ndiponso ziŵiya ndi zopereka za ku Nyumba ya Mulungu wathu zimene mfumu ndi aphungu ake ndi akalonga ake ndi Aisraele onse amene anali kumeneko, adaazipereka. Nditaziyesa zonse, ndidaŵapatsa m'manja mwao siliva wa matani 22, ziŵiya zasiliva za makilogaramu 70, ndiponso golide wa makilogaramu 3,400, mbale zagolide makumi aŵiri zolemera makilogaramu pafupi 8 ndi theka, ndiponso ziŵiya ziŵiri za mkuŵa wosalala wonyezemira bwino, zamtengowapatali wonga wa golide. Kenaka ndidaŵauza kuti, “Inu ndinu opatulika a Chauta, ndiponso mphatso zonsezi nzopatulika. Siliva ndi golideyu nzopereka zaufulu kwa Chauta, Mulungu wa makolo anu. Muzisamale ndi kuzisunga mpaka mutaziyesa pamaso pa akulu a ansembe, ndi Alevi, ndi akulu a mabanja a Aisraele, m'zipinda za m'Nyumba ya Chauta ku Yerusalemu.” Motero ansembe ndi Alevi adalandira siliva, golide ndi ziŵiya zoyesedwa zija, kuti apite nazo ku Yerusalemu ku Nyumba ya Mulungu wathu. Tsono tidachoka ku mtsinje wa Ahava pa tsiku la 12, pa mwezi woyamba, kupita ku Yerusalemu. Mulungu wathu anali nafe ndipo adatipulumutsa kwa adani athu, makamaka kwa anthu otibisalira pa njira. Tidafika ku Yerusalemu, ndipo tidatandala masiku atatu kumeneko. Pa tsiku lachinai lake, m'Nyumba ya Mulungu wathu momwemo, adayesa siliva ndi golide ndi ziŵiya zija, nkuzipereka m'manja mwa wansembe Meremoti, mwana wa Uriya. Pamodzi ndi iyeyo panali Eleazara mwana wa Finehasi, ndiponso Alevi aŵa: Yozabadi mwana wa Yesuwa, ndi Nowadiya mwana wa Biruyi. Zonsezo adaziŵerenga ndi kuziyesa ndipo adalemba kulemera kwa chinthu chilichonse. Nthaŵi imeneyo anthu amene adabwerako ku ukapolo, onse amene adaatengedwa aja, adapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu wa Israele, ng'ombe zamphongo khumi ndi ziŵiri, kuperekera Aisraele onse, nkhosa zamphongo 96, anaankhosa 77, ndiponso atonde 12, ngati nsembe yopepesera machimo ao. Zonsezo zinali nsembe zopsereza zopereka kwa Chauta. Iwowo adaperekanso chidziŵitso cha mfumu chija kwa akalonga a mfumu ndi kwa akazembe a m'dera la Patsidya pa Yufurate. Pamenepo iwowo adathandiza Ayuda ndiponso ntchito za pa Nyumba ya Mulungu. Zitachitika zimenezi, atsogoleri ena adadza kwa ine, nati, “Aisraele, ansembe ndi Alevi sadadzipatule kwa anthu a mitundu iyi yoyandikana nafe: Akanani, Ahiti, Aperezi, Ayebusi, Aamoni, Amowabu, Aejipito ndi Aamori. Anthu athuwo akuchita nawo zonyansa zaozo. Aisraele ena ndi ana ao aamuna adayamba kukwatira ana aakazi a anthuwo. Motero mtundu wathu wopatulika wadzisokoneza ndi mitundu ya anthu a m'maikowo. Ndipo atsogoleri ndi akuluakulu ndiwo amene akupambana pa kusakhulupirika kumeneku.” Nditamva zimenezi, ndidang'amba zovala zanga ndi mwinjiro wanga chifukwa cha chisoni, ndipo ndidazula tsitsi la kumutu kwanga ndi kumwetsula ndevu zanga, nkukhala pansi ndili wotaya mtima. Ndidakhala pansi choncho kufikira nthaŵi yamadzulo. Tsono anthu onse amene ankaopa mau a Mulungu wa Israele, ataona kusakhulupirika kwa obwerako ku ukapolo aja, adayamba kubwera kwa ine kudzasonkhana. Tsono itakwana nthaŵi ya nsembe yamadzulo, ndidadzidzimuka mumtima mwanga nkuimirira, zovala zanga zong'ambika zija zikali m'thupi. Ndidagwada nkukweza manja anga kwa Chauta, Mulungu wanga, Ndipo ndidati, “Inu Mulungu wanga, manyazi ndi chisoni zikundikanikitsa kukweza nkhope yanga kwa Inu Mulungu wanga, chifukwa zoipa zathu zakwera kopambana mitu yathu. Ndithu uchimo wathu wakwera mpaka kukafika kumwamba. Kuyambira nthaŵi ya makolo athu mpaka pano, takhala tikuchimwa kwambiri. Chifukwa cha machimo athuwo, ifeyo pamodzi ndi mafumu athu ndi ansembe athu, atipereka kwa mafumu a m'maiko achikunja, kuti atiphe pa nkhondo, atitenge ku ukapolo, atilande zinthu ndiponso kuti atichititse manyazi kwambiri, monga momwe ziliri masiku anomu. Koma tsopano pa kanthaŵi kochepaka, Inu Chauta, Mulungu wathu, mwaonetsa kukoma mtima kwanu. Mwalola kuti ena mwa ife tipulumuke ku ukapolo ndi kuloŵa m'malo anu oyera. Mwatilimbitsa mtima ndi kutitsitsimutsa kwa kanthaŵi mu ukapolo wathu. Inde ndife akapolo, komabe Inu Mulungu wathu simudatisiya mu ukapolo, mwatiwonetsa chikondi chanu chosasinthika pamaso pa mafumu a ku Persiya. Mwatitsitsimutsa kuti timange Nyumba yanu, Inu Mulungu wathu, pa mabwinja ake akale. Mwatitchinjiriza m'dziko la Yudeya ndiponso mu Yerusalemu. “Koma tsopano, Inu Mulungu wathu, ife tinganene chiyani titachita zoipa zonsezi? Taphwanya malamulo anu, amene mudatipatsa kudzera mwa aneneri atumiki anu. Mudaŵauza kuti, ‘Dziko mukuloŵamo kuti mulilandelo ndi dziko lodetsedwa ndi zonyansa za mitundu ya anthu a m'maikomo. Adzaza dziko lonselo ndi zoipa zaozo. Nchifukwa chake musakwatitse ana anu aakazi kwa ana ao aamuna, ndipo ana ao aakazi asakwatiwe ndi ana anu aamuna. Musakhale nawo mumtendere kapena kugwirizana nawo pa malonda, ngati mufuna kukhala amphamvu ndi kumadya zabwino za m'dzikomo, ndi kusiyira ana anu dziko limeneli kuti likhale choloŵa chao mpaka muyaya.’ Inde zonsezi zatigwera kaamba ka ntchito zathu zoipa ndi uchimo wathu waukulu. Komabe Inu Mulungu wathu, mwangotilanga pang'ono, kuyerekeza ndi kukula kwa kuchimwa kwathu, ndipo mwalola kuti ena mwa ife tipulumuke. Kodi ife nkuphwanyanso malamulo anu ndi kukwatirana ndi anthu a mitundu ina, amene amachita zonyansa zimenezi? Kodi simudzakwiya nafe ndi kutiwononga popanda wina wotsala, kapena wina aliyense wopulumuka? Inu Chauta, Mulungu wa Israele, ndinu achifundo pakuti ife ndife otsala amene tapulumuka, monga m'mene tiliri lero lino. Taima pano pamaso panu, tikuzindikira kuchimwa kwathu. Choncho palibe ndi mmodzi yemwe amene angaime pamaso panu chifukwa cha zochimwazi.” Pamene Ezara ankapemphera ndi kulapa, alikulira ndipo atadzigwetsa pansi ku Nyumba ya Mulungu, chinamtindi cha anthu chidabwera kwa iye kudzasonkhana. Panali amuna, akazi ndi ana, kuchokera m'dziko lonse la Israele, ndipo ankalira koopsa. Tsono Sekaniya, mwana wa Yehiyele, wa fuko la Elamu, adauza Ezara kuti, “Ife takhala osakhulupirika kwa Mulungu wathu, ndipo takhala tikukwatira akazi achilendo a mitundu ya m'maiko akunoŵa. Koma ngakhale zili choncho, chikhulupiriro chilipobe pakati pa Aisraele. Tiyeni tsono tichite naye chipangano Mulungu wathu, kuti ifeyo tilekane nawo akazi ameneŵa pamodzi ndi ana ao, potsata uphungu wa inu mbuyanga ndi wa anthu amene amaopa malamulo a Mulungu wathu. Ndipo tidzazichitadi potsata malamulowo. Ndiye inu dzukani, imeneyi ndi ntchito yanu, ndipo ife tili nanu. Valani dzilimbe ndipo muigwire ntchitoyo.” Choncho Ezara adanyamuka ndipo adalumbiritsa akulu a ansembe, Alevi ndi Aisraele onse, kuti adzachitedi monga m'mene Sekaniya adaanenera. Tsono onsewo adalumbira. Pambuyo pake Ezara adachokako ku Nyumba ya Mulungu napita ku chipinda cha Yehohanani, mwana wa Eliyasibu, kumene adakachezera usikuwo. Sadadye buledi kapena kumwa madzi. Nthaŵi yonseyo adakhalira kulira chifukwa cha kusakhulupirika kwa anthu obwerako ku ukapolo aja. Tsono anthu adalengeza m'dziko lonse la Yuda ndi mu mzinda wa Yerusalemu, kwa onse ochokera ku ukapolo aja, kuti asonkhane ku Yerusalemu. Adanena kuti, “Wina aliyense akapanda kufika asanathe masiku atatu, ndiye kuti potsata lamulo la atsogoleri ndi la akulu, adzayenera kumlanda katundu wake yense, ndipo adzachotsedwe m'gulu la anthu obwerako ku ukapolo aja.” Choncho anthu onse a m'dziko la Yuda ndi a m'dziko la Benjamini adasonkhana ku Yerusalemu asanathe masiku atatu. Limeneli linali tsiku la 20 la mwezi wachisanu ndi chinai. Ndipo anthu onse adakhala pansi pa bwalo la Nyumba ya Mulungu, ali njenjenje chifukwa cha nkhani imeneyi ndiponso chifukwa cha mvula yambiri imene inkagwa. Tsono wansembe Ezara adaimirira nati, “Mudachimwa pomakwatira akazi achikunja, ndipo mudaonjezera tchimo la Israele. Lapani tsopano kwa Chauta, Mulungu wa makolo anu, ndipo muchite zimene Iye akufuna. Dzichotseni pakati pa mitundu ya anthu a m'maiko enaŵa, ndi pa akazi achilendowo.” Chitamva mau amenewo, chinantindi chonse chapamsonkhanopo chidayankha mokweza mau kuti, “Ndi chonchodi, tiyenera kuchitadi monga mwaneneramo. Koma anthu ali panoŵa ngambiri, ndipo mvula ikugwa kwamphamvu, sitingathe kukaima pa mtetete. Chinanso nchakuti ntchitoyi si ya tsiku limodzi kapena masiku aŵiri, pakuti tidachimwa kwambiri pa nkhani imeneyi. Tsono atsogoleri athu aimirire m'malo mwa msonkhano wonse. Anthu onse a m'mizinda yathu amene adakwatira akazi achilendo abwere pa nthaŵi imene inu munene, ndipo abwere pamodzi ndi akulu ndi aweruzi a mzinda uliwonse. Motero mkwiyo woopsa wa Mulungu wathu pa nkhani imeneyi udzachoka.” Yonatani yekha, mwana wa Asahele, ndiponso Yahazeiya, mwana wa Tikiwa, ndi amene adatsutsapo pa zimenezi, ndipo Mesulamu pamodzi ndi Mlevi Sabetai, adaŵavomereza. Choncho anthu obwerako ku ukapolo aja, adachitadi momwemo. Wansembe Ezara adasankha anthu, akulu a mabanja potsata mafuko ao, aliyense kuchita kumlemba dzina. Pa tsiku loyamba la mwezi wakhumi, adayambapo kuifufuza nkhani imeneyi. Ndipo pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, anali atathana nawo anthu amene adaakwatira akazi achilendo aja. Nawu mndandanda wa ansembe amene adaakwatira akazi achilendo: Pa banja la Yesuwa ndi abale ake, ana a Yozadaki, panali aŵa: Maaseiya, Eliyezere, Yaribu ndi Gedaliya. Iwo adatsimikiza zochotsa akazi ao, ndipo adapereka nkhosa yamphongo yopepesera machimo ao. Pa banja la Imara panali Hanani ndi Zebadiya. Pa banja la Harimu panali Maaseiya, Eliya, Semaya, Yehiyele ndi Uziya. Pa banja la Pasuri panali Eliyoenai, Maaseiya, Ismaele, Netanele, Yozabadi ndi Elasa. Pakati pa Alevi panali aŵa: Yosabadi, Simei, Kelaya (amene ankatchedwanso Kelita), Petahiya, Yuda ndi Eliyezere. Pakati pa oimba nyimbo, panali Eliyasibu. Pakati pa alonda a ku Nyumba ya Mulungu panali Salumu, Telemu ndi Uri. Pakati pa Israele: a fuko la Parosi anali Ramiya, Iziya, Malikiya, Miyamini, Eleazara, Hasabiya ndi Benaya. A fuko la Elamu anali Mataniya, Zekariya, Yehiyele, Abidi, Yeremoti ndi Eliya. A fuko la Zatu anali Eliyoenai, Eliyasibu, Mataniya, Yeremoti, Zabadi, ndi Aziza. A fuko la Bebai anali Yehohanani, Hananiya, Zabibai ndi Atilai. A fuko la Bani anali Mesulamu, Malaki, Adaya, Yasubu, Seyala ndi Yeremoti. A fuko la Pahatimowabu anali Adina, Kelali, Benaya, Maaseiya, Mataniya, Bezalele, Binuyi ndi Manase. A fuko la Harimu anali Eliyezere, Isiya, Malikiya, Semaya, Simeoni Benjamini, Maluki ndi Semariya. A fuko la Hasumu anali Matenai, Matata, Zebadi, Elifeleti, Yeremai, Manase ndi Simei. A fuko la Bani anali Maadai, Amuramu, Uwele, Benaya, Bedeiya, Keluhu, Vaniya, Meremoti, Eliyasibu, Mataniya, Metenai, ndi Yasu. A fuko la Binuyi anali Simei, Selemiya, Natani, Adaya, Makinadebai, Sasai, Sarai, Azarele, Seremiya, Semariya, Salumu, Amariya ndi Yosefe. A fuko la Nebo anali Yeiyele, Matitiya, Zabadi, Zebina, Yadai, Yowele ndi Benaya. Onseŵa adaakwatira akazi achilendo. Tsono adaŵasudzula akaziwo pamodzi ndi ana ao omwe. Naŵa mau a Nehemiya, mwana wa Hakaliya: Pa mwezi wa Kisilevi, chaka cha 20 cha ufumu wa Arita-kisereksesi, pamene ndinali mu mzinda wa Susa, Hanani, mmodzi mwa abale anga, adabwera ndi anthu ena kuchokera ku Yuda. Ndipo ndidaŵafunsa za Yerusalemu ndiponso za Ayuda amene adaatsalirako osatengedwa ukapolo. Adandiyankha kuti, “Anthu amene aja ali pa mavuto ndiponso ali ndi manyazi aakulu. Makoma a Yerusalemu ngogamukagamuka, ndipo zipata zake zidaonongeka ndi moto.” Pamene ndidamva mau ameneŵa, ndidakhala pansi nkuyamba kulira, ndipo ndidalira masiku angapo. Ndinkasala chakudya, ndi kumapemphera kwa Mulungu wakumwamba. Ndidati, “Inu Chauta, Mulungu wakumwamba, Mulungu wamkulu ndi woopsa, mumasunga chipangano. Mumaonetsa chikondi chosasinthika kwa anthu amene amakukondani ndi kutsata malamulo anu. Tsekulani maso ndipo tcherani khutu, kuti mumve pemphero la mtumiki wanune, limene ndikupereka tsopano kwa Inu usana ndi usiku, kupempherera Aisraele atumiki anu. Ndikuvomera machimo amene ife Aisraele tidakuchimwirani. Zoonadi, ine pamodzi ndi banja la makolo anga, tidakuchimwirani. Tidakuchitirani zoipa zambiri, ndipo sitidamvere mau anu, malamulo anu ndiponso malangizo amene mudapatsa Mose mtumiki wanu. Kumbukirani mau amene mudauza Mose mtumiki wanu akuti, ‘Ngati mukhala osakhulupirika, ndidzakumwazani pakati pa anthu a mitundu ina. Koma mukabwerera kwa Ine, mukamvera malamulo anga ndi kuŵatsatadi, ndiye kuti ngakhale anthu anu omwazikawo akhale kutali chotani, ndidzaŵasonkhanitsa kuchokera ku mbali zonse ndi kubwera nawo ku malo amene ndidasankha kuti azidzandipembedza kumeneko.’ Iwoŵa ndiwo atumiki anu ndi anthu anu amene mudaŵapulumutsa ndi mphamvu yanu yaikulu ndi dzanja lanu lolimba. Inu Chauta, tcherani khutu kuti mumve pemphero la mtumiki wanune ndiponso pemphero la atumiki anu ena amene amakonda kulemekeza dzina lanu. Lolani kuti ine mtumiki wanu zinthu zindiyendere bwino lero, ndipo kuti mfumu indichitire chifundo.” Pa nthaŵi imeneyo nkuti ine ndili woperekera zakumwa kwa mfumu. Pa mwezi wa Nisani, chaka cha 20 cha ufumu wa Arita-kisereksesi, pamene adabwera ndi vinyo pamaso pa mfumuyo, ndidatenga vinyoyo ndi kumpereka kwa mfumu. Tsono nkale lonse sindidakhalepo ndi nkhope yachisoni pamaso pake. Apo mfumu idandifunsa kuti, “Kodi bwanji nkhope yako ili yakugwa, pamene sukudwala? Chimenechi si china, koma ndi chisoni chamumtima.” Pamenepo ndidaopa kwambiri. Ndidauza mfumu kuti, “Amfumu akhale ndi moyo mpakampaka. Ilekerenji nkhope yanga kukhala yakugwa, pamene mzinda kumene kuli manda a makolo anga, adani adausandutsa bwinja, ndipo zipata zake adazitentha ndi moto?” Tsono mfumu idandifunsa kuti, “Tsono umati undipemphe chiyani?” Pamenepo ndidapemphera kwa Mulungu Wakumwamba. Ndipo ndidaiwuza mfumuyo kuti, “Ngati chingakukondweretseni amfumu, ndipo ngati mungandikomere mtima mtumiki wanune, munditume ku Yuda, kumzinda kumene kuli manda a makolo anga, kuti ndikaumangenso mzindawo.” Apo mfumu, mkazi wake ali pambali pake, idandifunsa kuti, “Kodi kumeneko ukakhalako nthaŵi yaitali bwanji, ndipo udzabwerako liti?” Ndidaiwuza nthaŵi yake, ndipo idandilola kuti ndipite. Tsono ndidauza mfumu kuti, “Ngati chingakukondweretseni amfumu, mundipatse makalata oti ndikapereke kwa abwanamkubwa a chigawo cha Patsidya pa Yufurate, kuti akandilole kudzera m'chigawocho mpaka ndikafike ku Yuda. Mundipatsenso kalata ina yolembera Asafu, kapitao woyang'anira nkhalango ya mfumu, kuti akandipatse mitengo yokamangira mitanda ya zipata za linga loteteza Nyumba ya Mulungu, ya makoma a mzinda, ndiponso ya nyumba yokakhalamo ine.” Mfumu idandipatsa zimene ndidaapemphazo, popeza kuti Mulungu wanga wokoma mtima anali nane. Choncho ndidanyamuka ulendo nkukafika kwa abwanamkubwa a chigawo cha Patsidya pa Yufurate, ndipo ndidaŵapatsa makalata a mfumu aja. Monsemo nkuti mfumu itatumiza akulu ankhondo ndiponso anthu okwera pa akavalo, kuti atsakane nane. Koma atamva zimenezi, akuluakulu aŵa, Sanibalati wa ku Horoni ndi Tobiya, mkulu wina wa chigawo cha Amoni, adaipidwa kwambiri poona kuti wina wabwera kudzachitira Aisraele zabwino. Choncho ndidafika ku Yerusalemu ndipo ndidakhala kumeneko masiku atatu. Sindidauze ndi mmodzi yemwe zimene Mulungu wanga adaaika mumtima mwanga, zoti ndichitire Yerusalemu. Tsono ndidadzuka usiku pamodzi ndi anthu ena oŵerengeka. Ndinalibe bulu wina kupatula yekhayo amene ndidaakwerapo. Ndidatuluka usiku podzera ku Chipata cha ku Chigwa, nkuyenda cha ku Chitsime cha Chilombo Cham'madzi ndi ku Chipata cha Zinyalala. Ndipo ndidayang'ana makoma a Yerusalemu amene adaagamukagamuka ndiponso zipata zake zimene zidaaonongeka ndi moto. Pambuyo pake ndidapitirira mpaka kukafika ku Chipata cha Kasupe ndi ku Dziŵe la Mfumu. Koma panalibe malo oti bulu amene ndidaakwerapoyo adzerepo. Choncho ndidayenda ndi usiku kudzera ku chigwa, kunka ndikuliyang'ana khomalo. Ndipo ndidapotoloka nkudzaloŵa mu mzinda kudzera pa Chipata cha ku Chigwa chija. Akuluakulu aja sadadziŵe kumene ndidaapita kapenanso zimene ndinkachita. Ndinali ndisanaŵauze Ayuda, ansembe, atsogoleri, akuluakulu aja kapenanso ena onse amene ankayenera kudzagwira ntchitoyo. Tsono ndidaŵauza kuti, “Mukuwona mavuto amene tili nawo. Yerusalemu wasanduka bwinja ndipo zipata zake azitentha. Tiyeni timange makoma a Yerusalemu, kuti tisamachitenso manyazi.” Motero ndidaŵasimbira za m'mene Mulungu wanga adandithandizira ndiponso mau amene mfumu idandiwuza. Apo anthuwo adati, “Tiyeni tiyambepo kumanga.” Choncho adalimbitsana mtima kuti akaiyambe ntchito yabwinoyo. Koma pamene akuluakulu aja Sanibalati ndi Tobiya ndiponso Gesemu Mwarabu adamva zimenezi, adayamba kutiseka ndi kutinyoza. Adati, “Kodi chimene mukuchitachi nchiyani? Mukuti muukire mfumu kodi?” Ine ndidaŵayankha kuti, “Mulungu Wakumwamba adzatithandiza kuti zinthu zitiyendere bwino, ndipo ife atumiki ake tiyambapo kumanga. Koma inuyo mulibe chanu muno, mulibe mphamvu yolandirira malo muno, ndipo mulibenso chilichonse chokumbutsa za inu mu Yerusalemu.” Pambuyo pake Eliyasibu, mkulu wa ansembe, adayamba kugwira ntchito pamodzi ndi ansembe anzake, ndipo adamanga Chipata cha Nkhosa. Adachipatulira Mulungu naika zitseko zake. Khoma limene adapatulalo lidafika ku Nsanja ya Zana, mpakanso ku Nsanja ya Hananele. Anthu a ku Yeriko adamanga chigawo china pambalipa, ndipo Zakuri, mwana wa Imuri, adamanga chigawo chinanso kuyandikana ndi chimenechi. A fuko la Hasena adamanga Chipata cha Nsomba. Iwowo adayala mitanda yake naikira zitseko zake, zotsekera zake, ndi mipiringidzo yake. Pambali pa iwowo Meremoti, mwana wa Uriya, mwana wa Hakozi, adakonza chigawo china. Pambali pa iwowo Mesulamu, mwana wa Berekiya, mwana wa Mesezabele, adakonza chigawo china. Pambali pa iwowo Zadoki, mwana wa Baana, adakonza chigawo china. Pambali pa iwowo Atekowa adakonza chigawo china, koma atsogoleri ao adakana kugwira ntchito imene akuluakulu ao adaŵapatsa. Yoyada, mwana wa Paseya, ndi Mesulamu mwana wa Besodeiya, adakonza Chipata Chakale. Adayala mitanda yake naikira zitseko zake, zotsekera zake ndi mipiringidzo yake. Pambali pa iwowo, Melatiya Mgibiyoni ndi Yadoni Mmeronoti, ndiponso anthu a ku Gibiyoni ndi a ku Mizipa, adakonza chigawo chao mpaka ku nyumba ya bwanamkubwa wa chigawo cha Patsidya pa Yufurate. Pambali pa iwowo Uziyele, mwana wa Haraiya, wa m'gulu la amisiri osula golide, adakonza chigawo china. Pambali pa iyeyo Hananiya, mmodzi mwa anthu oyenga mafuta onunkhira, adakonza chigawo china. Onsewo adakonza Yerusalemu mpaka ku Khoma Lotambasuka. Pambali pa iwowo Refaya, mwana wa Huri, wolamulira theka la dera la mzinda wa Yerusalemu, adakonza chigawo china. Pambali pa iwowo Yedaya, mwana wa Harumafa, adakonza chigawo choyang'anana ndi nyumba yake. Pambali pa iyeyo Hatusi, mwana wa Hasabuneiya, adakonza chigawo china. Malikiya, mwana wa Harimu, ndiponso Hasubu mwana wa Pahatimowabu, adakonza chigawo china pamodzi ndi Nsanja ya Ng'anjo. Pambali pa iyeyo Salumu, mwana wa Halohesi, wolamulira theka lina la dera la mzinda wa Yerusalemu, adakonza chigawo china, iyeyo pamodzi ndi ana ake aakazi. Hanuni pamodzi ndi nzika za ku Zanowa adakonza Chipata cha ku Chigwa. Adachimanganso naikira zitseko zake, zotsekera zake ndi mipiringidzo yake. Adakonzanso khoma mamita 400 mpaka kukafika ku Chipata cha Zinyalala. Malakiya, mwana wa Rekabu, wolamulira dera la Betehakeremu, adakonza Chipata cha Zinyalala. Adachimanganso, naikira zitseko zake, zotsekera zake ndi mipiringidzo yake. Salumu mwana wa Kolihoze wolamulira dera la Mizipa, adakonza Chipata cha Kasupe. Adachimanganso, naikira denga lake, zitseko, zotsekera ndi mipiringidzo yake. Adamanganso khoma la Dziŵe la Sela pafupi ndi munda wa mfumu, mpaka ku makwerero otsikira potuluka mu mzinda wa Davide. Pambali pa iyeyo Nehemiya, mwana wa Azibuki, wolamulira theka la dera la Betezuri, adakonza chigawo china mpaka ku malo oyang'anana ndi manda a Davide, ndi kukafika ku dziŵe lokumba ndiponso ku nyumba ya ankhondo. Pambali pa Nehemiyayo Alevi adakonza chigawo china. Mtsogoleri wao anali Rehumu mwana wa Bani. Pambali pa iyeyo Basabiya, wolamulira theka la dera la Keila, adakonza chigawo chake. Pambali pa iyeyo abale ao adapitiriza kukonza. Mtsogoleri wao anali Bavai mwana wa Henadadi, wolamulira theka la dera lina la Keila. Pambali pa iyeyo Ezere mwana wa Yesuwa wolamulira Mizipa, adakonza chigawo china choyang'anana ndi chikweza chofikira ku malo osungira zida zankhondo pa Ndonyo. Pambali pa iyeyo Baruki mwana wa Zabai adakonza chigawo kuyambira pa Ndonyo mpaka ku chitseko cha nyumba ya Eliyasibu, mkulu wa ansembe. Pambali pa iyeyo Meremoti mwana wa Uriya, mwana wa Hakozi, adakonza chigawo china kuyambira ku chitseko cha nyumba ya Eliyasibu mpaka ku mathero a nyumbayo. Pambali pa Meremoti, ansembe okhala ku chidikha adakonza chigawo china. Pambali pa iwowo Benjamini ndi Hasubu adakonza chigawo china choyang'anana ndi nyumba zao. Pambali pa iwowo Azariya, mwana wa Maaseiya, mwana wa Ananiya, adakonza chigawo china pafupi ndi nyumba yake. Pambali pa iyeyo Binuyi, mwana wa Henadadi, adakonza chigawo china, kuyambira ku nyumba ya Azariya mpaka kukafika ku Ndonyo, ndiponso mpaka ku ngodya. Palala, mwana wa Uzai, adakonza chigawo china choyang'anana ndi Ndonyo ndiponso ndi nsanja yotuluka pa nyumba yapamwamba ya mfumu ku bwalo la alonda. Pambali pa iyeyo Pedaya, mwana wa Parosi, ndi atumiki a ku Nyumba ya Mulungu, amene ankakhala pa khoma la Ofele, adakonza chigawo china mpaka ku malo oyang'anana ndi Chipata cha Madzi kuvuma, ndiponso nsanja yaitali ija. Pambali pa Pedaya ndi anzake, Atekowa adakonza chigawo china choyang'anana ndi nsanja ija yaikulu ndi yaitali mpaka kukafika ku khoma la Ofele. Kuyambira ku Chipata cha Akavalo, ansembe ena ankakonza khoma, aliyense moyang'anana ndi nyumba yake. Pambali pa iwowo Zadoki, mwana wa Imeri, adakonza chigawo china choyang'anananso ndi nyumba yake. Pambali pa iyeyo Semaya, mwana wa Sekaniya, amene ankasunga Chipata chakuvuma, adakonza chigawo china. Pambali pa iyeyo Hananiya, mwana wa Selemiya, ndiponso Hanuni, mwana wachisanu ndi chimodzi wa Zalafi, adakonza chigawo china. Pambali pa iwowo Mesulamu, mwana wa Berekiya, adakonza chigawo choyang'anana ndi chipinda chake. Pambali pa iyeyo Malikiya, mmodzi mwa amisiri a golide, adakonza chigawo china mpaka kukafika ku nyumba ya atumiki a ku Nyumba ya Mulungu, ndiponso ku nyumba ya anthu amalonda. Chigawo chimenechi chidaayang'anana ndi Chipata cha Mifikada, kufikira ku chipinda chapamwamba chapangodya. Ndipo pakati pa chipinda chapamwamba chapangodya ndi Chipata cha Nkhosa, amisiri a golide ndi anthu amalonda adakonza chigawo chao. Pamene Sanibalati adamva kuti tikumanga khoma, adapsa mtima nakalipa kwambiri, ndipo adayamba kuŵaseka Ayuda monyodola. Adalankhula pamaso pa abale ake, ndi pamaso pa gulu lankhondo la ku Samariya, adati, “Kodi Ayuda achabechabeŵa akuchita chiyani? Monga amati nkumanganso mzindawu? Kodi nsembe ndiye adzapereka? Kodi adzaumaliza pa tsiku limodzi? Kodi adzachita kutolatolanso miyala yakale ija, ndi m'mene idapsera muja?” Tobiya Mwamoni amene anali naye adati, “Inde, chimene akumangacho, ngati nkhandwe ikwerapo, idzagwetseratu khoma la miyala laolo.” Pamenepo ndidayamba kupemphera, ndidati, “Inu Mulungu wathu, imvani m'mene akutinyozera. Mau ao otonza aŵabwerere, anthu ameneŵa alandidwe zao zonse, ndipo atengedwe ukapolo ku dziko lachilendo. Musaŵakhululukire cholakwa chao, musafafanize tchimo lao, popeza kuti aputa ukali wanu pamaso pa amisiri omanga.” Motero tidamangabe khoma, ndipo khoma lonse tidatha kulimanga mpaka theka la msinkhu wake, chifukwa chakuti anthu adaaikapo mtima pa ntchitoyo. Koma pamene Sanibalati ndi Tobiya, ndiponso Arabu, Aamoni ndi Aasidodi adamva kuti ntchito yokonza makoma a Yerusalemu ikupita m'tsogolo, ndipo kuti malo ogamukagamuka aja akuŵakonzanso, adapsa mtima kwambiri. Tsono adapangana za chiwembu choti akathire nkhondo Yerusalemu ndi kusokoneza anthu amumzindamo. Apo ife tidapemphera kwa Mulungu wathu, ndipo tidaika alonda oti azititeteza kwa adani athuwo usana ndi usiku. Tsono Ayuda ankati, “Mphamvu za onyamula zinyalala zilikutha, ndipo zinyalala zoyenera kutayidwazo nzambiri. Ndiyetu sitiitha ife ntchito yomanga khomayi.” Adani athu ankanena zakuti ife Ayuda sitidzadziŵa kapena kuwona kanthu, mpaka iwo atafika pakati pathu, natipha ndi kuletsa ntchito yathuyi. Tsono Ayuda okhala pafupi ndi adani athuwo ankabwera natichenjeza kakhumi konse kuti “Iwo aja adzafika kudzalimbana nanu kuchokera kulikonse kumene amakhala.” Choncho paliponse pamene khomalo linali lisanathe, kumbuyo kwake, cha m'munsi mwake, m'malo okonza bwino, ndidaikamo anthu, m'mabanjam'mabanja, atatenga malupanga, mikondo ndi mauta. Koma nditazindikira mantha ao, ndidachitapo kanthu. Mwakuti ndidauza atsogoleri ndi akulu olamula, ndiponso anthu ena onse kuti, “Musaŵaope ameneŵa. Kumbukirani kuti Chauta ndi wamkulu ndiponso ndi woopsa, tsono mumenyere nkhondo abale anu, ana anu, akazi anu, ndi nyumba zanu.” Pamene adani athu adamva kuti ife tikudziŵa cholinga chao, adazindikira kuti Mulungu walepheretsa zimene iwowo adaapangana kuti atichite. Tsono tonse tidapitanso ku ntchito yomanga khoma, aliyense ku ntchito yake. Kuyambira tsiku limenelo mpaka m'tsogolo mwake, theka lina la antchito anga linkagwira ntchitoyo, ndipo theka lina linkagwira mikondo, zishango, mauta ndiponso linkavala malaya achitsulo. Tsono akulu a Ayuda ankalimbitsa anthu ao amene ankamanga khoma. Anthu onyamula zinyalala aja ankagwira ntchito ndi dzanja limodzi, kwinaku atagwira chida chankhondo. Mmisiri aliyense anali atamangirira lupanga m'chiwuno mwake pamene ankamanga. Munthu woimba lipenga anali pambali panga nthaŵi zonse. Ndidaŵauza atsogoleri ndi akuluakulu ndiponso anthu ena onse aja kuti, “Ntchitoyi njaikulu, ili pa dera lalikulu, ndipo ifeyo takhala motayanatayana kwambiri pa khoma. Tsono kumene muliriko mukamva kulira kwa lipenga, mudzasonkhane msanga kumene tili ife kuno. Mulungu wathu adzatimenyera nkhondo.” Choncho enafe tinkagwira ntchito, ndipo theka lina la anthuwo linkagwira zida zankhondo, kuyambira m'matandakucha mpaka nyenyezi zitaoneka. Pa nthaŵi imeneyi ndidaŵauzanso anthu kuti, “Aliyense pamodzi ndi wantchito wake agone m'Yerusalemu, kuti tikhale ndi otitchinjiriza usiku, ndipo kuti masana tizigwira ntchito.” Motero ine, anzanga, antchito anga, ndiponso anthu otitchinjiriza amene ankanditsata, panalibe ndi mmodzi yemwe mwa ife amene ankavula zovala zake usiku pogona. Aliyense ankasunga chida chankhondo pambalipa. Tsono anthu ena pamodzi ndi akazi ao adayamba kudandaula kwambiri chifukwa cha Ayuda anzao. Pakuti panali ena amene ankati, “Ife ndi ana athu tikuchuluka kwambiri, motero tikusoŵa tirigu wakudya, kuti tikhale ndi moyo.” Panalinso ena amene ankati, “Ife tikuchita kupereka minda yathu, mitengo yathu yamphesa, pamodzi ndi nyumba zathu, ngati chikole, kuti tipeze tirigu, poti njala yatipha.” Panali enanso amene ankati, “Ife tachita kukongola ndalama kuti tikhome msonkho wa minda yathu kwa mfumu, ndiponso kuti tikhomere mitengo yathu yamphesa. Tsonotu ife ndi anzathu aja ndife amodzi, ndipo ana athu ngofanafana ndi ana ao. Komabe ifeyo tikukakamiza ana athu kuti akhale akapolo, mwakuti ana athu ena aakazi agwidwa kale. Ifeyo tilibe mphamvu zoti nkuchitapo kanthu, poti anthu aja atenga kale minda yathu ndi mitengo yathu yamphesa.” Ine nditamva madandaulo amenewo, ndidapsa mtima kwambiri. Ndidatsimikiza kuti ndichitepo kanthu, ndipo ndidaŵadzudzula atsogoleri ndi akulu olamula omwe. Ndidati, “Kodi nzokuwonerani kuti mukulipitsana chiwongoladzanja anthu apachibale nokhanokha!” Pamenepo ndidachititsa msonkhano waukulu kuti ndiŵazenge mlandu. Tsiku limenelo ndidaŵauza kuti, “Monga m'mene kwathekera, tayesetsa kuwombola abale athu, Ayuda amene adaagulitsidwa ngati akapolo kwa anthu a mitundu ina. Koma tsopano inu mukugulitsa ngakhale abale anu omwe kwa anzao, kuti ife tiwumirizidwe kuŵaombola.” Anthuwo adangokhala chete osaona ponena. Tsono ine ndidaonjeza kuti, “Zimene mukuchitazi si zabwinotu ai. Muziwopa Mulungu ndi kumachita zolungama, kuti adani athu a mitundu inaŵa asapeze chifukwa chotinyozera. Chinanso nchakuti ine, pamodzi ndi abale anga ndiponso antchito anga, tidaŵakongoza ndalama ndi tirigu. Tiyeni tisaŵaumirize kubwezera ngongolezo. Muŵabwezere lero lomwe lino minda yao, mitengo yao yamphesa, mitengo yao ya olivi, ndi nyumba zao, ndipo muŵakhululukire ngongole za ndalama, za tirigu, za vinyo, ndi za mafuta, zimene mudaaŵakongoza.” Ndiye iwowo adayankha kuti, “Tidzachitadi monga mukuneneramu. Tidzabwezera zimenezi osapemphapo kanthu.” Pamenepo ndidaitana ansembe, ndipo pamaso pao ndidaŵalumbiritsa akuluwo kuti adzachitedi monga momwe adalonjezera. Tsono ndidakutumula chovala changa ndipo ndidanena kuti, “Chimodzimodzinso Mulungu akutumule munthu aliyense wosasunga malonjezo akeŵa. Amsandutse mmphaŵi pakumlanda nyumba yake, antchito ake ndi zonse zimene ali nazo.” Apo msonkhano wonse udavomereza ponena kuti, “Zikhale momwemo ndithu!” Ndipo onsewo adatamanda Chauta. Pambuyo pake akulu aja adachita monga m'mene adaalonjezera. Kuyambiranso nthaŵi imene adandisankha kuti ndikhale bwanamkubwa m'dziko la Yuda, kuchokera chaka cha 20 mpaka chaka cha 32 cha ufumu wa Arita-kisereksesi, ndiye kuti zaka khumi ndi ziŵiri, ineyo ndi abale anga sitidalandire chakudya choyenerera bwanamkubwa. Abwanamkubwa amene analipo kale ankasautsa anthu pomaŵalanda chakudya ndi vinyo, ndi kuŵalipitsanso masekeli asiliva makumi anai. Ngakhale antchito ao nawonso ankathinitsa anthu. Koma ine sindidachite nawo zimenezo, popeza kuti ndinkaopa Mulungu. Ndiponso ndinkakangamira pa ntchito yomanga makoma a mzinda, osafuna kupata minda. Antchito anga onsenso anali komweko, ndidaaŵalamula kuti adzipereke pa ntchito yokhayokhayo. Komanso masiku onse ndinkadyetsa anthu 150, Ayuda ndi akulu olamula, kuphatikizapo anthu amene adaabwera kwa ife kuchokera kwa mitundu ina yotizungulira. Tsono chakudya cha pa tsiku limodzi chinali ichi: ng'ombe imodzi, nkhosa zisanu ndi imodzi zonenepa, ndiponso nkhuku zochuluka. Pa masiku khumi aliwonse panalinso matumba achikopa ochuluka a vinyo. Komabe ngakhale choncho, ine sindidafune kulandira chakudya chimene abwanamkubwa ankalandira, chifukwa chakuti anthu anga anali othinidwa kwambiri. Kuti tipeze bwino, kumbukirani, Inu Mulungu wanga, zonse zimene ndidaŵachitira anthuzi. Kudangotero kuti Sanibalati, Tobiya, Gesemu Mwarabu ndiponso adani athu ena adamva kuti tidatha kumanganso khoma, ndipo kuti sipadatsale mpamodzi pomwe pogumuka, ngakhale tinali tisanaike zitseko pa zipata. Tsono Sanibalati ndi Gesemu adanditumizira mau onena kuti, “Mubwere, tidzakumane pa mudzi wina m'chigwa cha Ono.” Ankafuna kukandichita chiwembu kumeneko. Nchifukwa chake ndidaŵatumira amithenga kukaŵauza kuti, “Ine kuno ndili pa ntchito yaikulu, sindingathe kuchoka kuti ndibwere kumeneko. Kodi ntchito iime, pofuna kuti ndibwere kumeneko?” Tsono adanditumizira mau okhaokhawo kanai konse, ndipo ndidaŵayankha chimodzimodzi. Pamenepo Sanibalati adatumanso wantchito wake kachisanu kwa ine. Iye anali ndi kalata yosamata m'manja mwake. M'kalatamo munali mau akuti, “Pakati pa mitundu ya anthu pano pamveka mphekesera, ndiponso Gesemu akunenanso momwemo, kuti inuyo, pamodzi ndi Ayuda, mukufuna kuukira boma. Nchifukwa chake mukumanganso khoma. Mukufuna kuti mukhale mfumu yao monga m'mene zikumvekeramu. Mwaikanso aneneri ku Yerusalemu oti azilengeza za inu kuti, ‘Ku Yuda kuli mfumu tsopano!’ Tsono zonsezi zimveka ndithu kwa mfumu ya ku Persiya. Choncho mubwere kuti tidzakambirane tonse pamodzi.” Apo ndidamtumizira mau akuti, “Pa zimene mukunenazi, palibe chimene chidachitikapo. Zonsezi mukungoziganiza nokha.” Ndidaazindikira kuti adaniwo ankangofuna kutiwopsa, namaganiza kuti, “Ayudaŵa adzachita mantha ndipo adzaleka kugwira ntchito, motero ntchitoyo siidzatha.” Koma ine ndidapemphera kuti, “Inu Mulungu, tsopano mundilimbitse mtima.” Nthaŵi imeneyo ndidapita ku nyumba ya Semaya, mwana wa Delaya, mwana wa Mehetabele, amene sankatuluka m'nyumba mwake. Iye adandiwuza kuti, “Tiyeni tikabisale m'Nyumba ya Mulungu, tikatsekeko pakuti akubwera kudzakuphani. Ndithudi, akubwera usiku kudzakuphani.” Koma ine ndidayankha kuti, “Munthu wonga ine nkuthaŵa kodi? Ndipo munthu wonga ine, kodi nkukabisala m'Nyumba ya Mulungu, kuti ndidzipulumutse? Zimenezo ai, toto, ine sindipitako!” Kenaka ndidazindikira kuti Mulungu sadamtume, koma ankandinenera zimenezi chifukwa chakuti Tobiya ndi Sanibalati ndiwo adaamlemba ntchito imeneyi. Chimene adaamlembera ntchitoyo nkuti andichititse mantha, ineyo ndithaŵe. Motero ndikadachimwa, ndipo iwowo akadandiipitsira mbiri kuti azidzandinyodola. Pamenepo ndidapemphera kuti, “Inu Mulungu wanga, kumbukirani zimene Tobiya ndi Sanibalati adachita. Kumbukiraninso zimene mneneri wamkazi Nowadiya ndiponso aneneri ena aja ankachita pofuna kundichititsa mantha.” Patapita masiku 52, pa tsiku la 25 la mwezi wa Eluli, khoma lija adatsiriza kumanga. Adani athu onse a m'madera oyandikana nafe atamva zimenezi, adachita mantha kwambiri. Adachita manyazi pakuti iwo adaazindikira kuti ntchitoyo yachitika ndi chithandizo cha Mulungu wathu. Kuwonjezera apo, nthaŵi imeneyo atsogoleri a ku Yuda ankalemberana makalata ndi Tobiya, pakuti anthu ambiri ku Yuda adaalumbira kuti adzagwirizana naye, chifukwa chakuti anali mkamwini wa Myuda mnzao, Sekaniya, mwana wa Ara. Ndipo mwana wake, Yehohanani, anali atakwatira mwana wamkazi wa Mesulamu, mwana wa Berekiya. Anthu ankasimba za ntchito zabwino za Tobiyayo ine ndili pomwepo, ndipo ankamuululira mau anga. Choncho iyeyo ankalemba makalata ondichititsa mantha aja. Khoma la mzinda lija litamangidwa, ndidaikira zitseko, ndipo alonda a ku Nyumba ya Mulungu, anthu oimba nyimbo ndiponso Alevi adasankhidwa. Pamenepo ndidasankha mbale wanga Hanani ndi Hananiya, mkulu woyang'anira linga lankhondo, kuti aŵiriwo azilamulira Yerusalemu. Hananiyayo anali munthu wokhulupirika ndi womvera Mulungu kupambana anthu ambiri. Tsono ndidaŵauza kuti, “Musalole kuti atsekule zipata za Yerusalemu mpaka dzuŵa litatentha. Ndipo atseke zitseko ndi kuzipiringidza, alonda asanaŵeruke. Musankhe olonda pakati pa anthu okhala m'Yerusalemu, aliyense akhale pamalo pake, ndiponso akhale poyang'anana ndi nyumba yake.” Mzinda wa Yerusalemu unali wotambasuka ndiponso waukulu, koma anthu okhala mumzindamo anali oŵerengeka, ndipo munalibe nyumba zambiri. Tsono Mulungu adaika mumtima mwanga maganizo oti ndisonkhanitse atsogoleri, akuluakulu ndiponso anthu onse, kuti alembedwe potsata mibadwo ya mabanja ao. Ndidapeza buku m'mene mudalembedwa maina a mabanja a anthu amene anali oyamba kubwerako ku ukapolo. Zolembedwa m'menemo zinali izi: Naŵa anthu a m'chigawo cha Yuda amene adabwerako ku ukapolo, omwe Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adaaŵagwira kupita nawo ku Babiloni. Anthuwo adabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wa makolo ake. Adabwera pamodzi ndi atsogoleri aŵa: Zerubabele, Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Mordekai, Bilisani, Misipereti, Bigivai, Nehumu ndi Baana. Nachi chiŵerengero cha anthu aamuna a Aisraele. A banja la Parosi 2,172. A banja la Sefatiya 372. A banja la Ara 652. A banja la Pahatimowabu, ndiye kuti zidzukulu za Yesuwa ndi Yowabu 2,818. A banja la Elamu 1,254. A banja la Zatu 845. A banja la Zakai 760. A banja la Binuyi 648. A banja la Bebai 628. A banja la Azigadi 2,322. A banja la Adonikamu 667. A banja la Bigivai 2,067. A banja la Adini 655. A banja la Atere, ndiye kuti la Hezekiya, 98. A banja la Hasumu 328. A banja la Bezai 324. A banja la Harifi 112. A banja la Gibiyoni 95. Amuna a ku Betelehemu ndi a ku Netofa 188. Amuna a ku Anatoti 128. Amuna a ku Betazimaveti 42. Amuna a ku Kiriyati-Yearimu, Kefira, ndi Beeroti 743. Amuna a ku Rama ndi Geba, 621. Amuna a ku Mikimasi 122. Amuna a ku Betele ndi Ai 123. Amuna a ku Nebo wina 52. A banja la Elamu wina 1,254. A banja la Harimu 320. A ku Yeriko 345. A ku Lodi, Hadidi ndi Ono 721. A ku Senaya 3,930. Ansembe anali aŵa: a banja la Yedaya, ndiye kuti zidzukulu za Yesuwa, 973. A banja la Imara 1,052. A banja la Pasuri 1,247. A banja la Harimu 1,017. Alevi anali aŵa: a banja la Yesuwa ndi la Kadimiyele, ndiye kuti zidzukulu za Hodaviya, 74. Oimba nyimbo anali aŵa: a banja la Asafu 148. Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali aŵa: a banja la Salumu, a banja la Atere, a banja la Talimoni, a banja la Akubu, a banja la Hatita, a banja la Sobai, onse pamodzi 138. Antchito a ku Nyumba ya Mulungu anali aŵa: a banja la Ziha, a banja la Hasufa, a banja la Tabaoti, a banja la Kerosi, a banja la Siya, a banja la Padoni, a banja la Lebana, a banja la Hagaba, a banja la Salimai, a banja la Hanani, a banja la Gidele, a banja la Gahara, a banja la Reaya, a banja la Rezini, a banja la Nekoda, a banja la Gazamu, a banja la Uza, a banja la Paseya, a banja la Besai, a banja la Meunimu, a banja la Nefusesimu, a banja la Bakibuki, a banja la Hakufa, a banja la Harihuri, a banja la Baziliti, a banja la Mehida, a banja la Harisa, a banja la Barikosi, a banja la Sisera, a banja la Tema, a banja la Neziya, a banja la Hatifa. Mabanja a antchito ake a Solomoni anali aŵa: a banja la Sotai, a banja la Sofereti, a banja la Perida, a banja la Yaala, a banja la Darikoni, a banja la Gidele, a banja la Sefatiya, a banja la Hatili, a banja la Pokereti-Hazebaimu ndi a banja la Amoni. Antchito onse a ku Nyumba ya Mulungu, kuphatikizapo zidzukulu za antchito a Solomoni, onse pamodzi analipo 392. Anthu ali m'munsiŵa ndiwo amene adabwera kuchokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adoni ndi ku Imeri, ngakhale sankatha kutsimikiza kuti makolo ao kapena mafuko ao analidi Aisraele enieni kapena ai. A banja la Delaya, a banja la Tobiya, a banja la Nekoda 642. Ndiponso ena mwa ansembe anali aŵa: a banja la Hobaya, a banja la Hakozi, a banja la Barizilai (kunena amene adaakwatira mmodzi mwa ana aakazi a Barizilai wa ku Giliyadi, nkutenga dzina la bambo waoyo). Iwoŵa adaafunafuna maina ao m'buku lolongosola kaundula wa mafuko ao, koma maina ao sadapezekemo. Choncho adaŵachotsa pa unsembe naŵaŵerenga kuti ngodetsedwa pa chipembedzo. Bwanamkubwa adaŵauza anthuwo kuti asamadye nawo chakudya choperekedwa kwa Mulungu, mpaka wansembe wodziŵa kuwombeza ndi Urimu ndi Tumimu atapezeka. Chiŵerengero cha anthu onse obwerako ku ukapolo aja chinali 42,360. Kuwonjezera pamenepa, panalinso antchito ao aamuna ndi aakazi okwanira 7,337. Anali nawonso anthu oimba nyimbo, amuna ndi akazi omwe, okwanira 245. Akavalo ao analipo 736, nyulu zao zinalipo 245, ngamira zao zinalipo 435, ndipo abulu ao analipo 6,720. Atsogoleri ena a mabanja adapereka mphatso zothandizira ntchito. Bwanamkubwa adapereka ku thumba la chuma ndalama zagolide za makilogaramu asanu ndi atatu, mbale makumi asanu, ndiponso mikanjo ya ansembe yokwanira 530. Atsogoleri ena a mabanja adapereka mosungira chumamo ndalama zagolide za makilogaramu 168, ndiponso ndalama zasiliva za makilogaramu 1,250. Ndipo anthu onse otsala adapereka ndalama zagolide za makilogaramu 168, ndalama zasiliva zamakilogaramu 140, ndiponso mikanjo ya ansembe yokwanira 67. Motero ansembe, Alevi, alonda a ku Nyumba ya Mulungu, anthu oimba nyimbo, ambiri mwa anthu wamba, atumiki a m'Nyumba ya Mulungu ndi Aisraele ena onse, ankakhala m'mizinda mwao. Ndipo anthu onse adasonkhana pamodzi pa bwalo la patsogolo pa Chipata cha Madzi. Tsono anthuwo adamuuza Ezara, amene anali mlembi, wansembe ndi mphunzitsi wa malamulo, kuti abwere ndi buku la Malamulo a Mose limene Chauta adaapatsa Israele. Pamenepo Ezarayo adabwera ndi buku la Malamulolo, pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiŵiri, ku msonkhano wa amuna ndi akazi ndi ana amene ankatha kumvetsa zinthu bwino. Tsono Ezara adaŵerenga bukulo atayang'ana bwalo la Chipata cha Madzi, kuyambira m'mamaŵa mpaka pa masana, pamaso pa amuna ndi akazi omwe, ndiponso onse amene ankatha kumvetsa zinthu bwino. Ndipo anthu onsewo ankatchera makutu kuti amve zoŵerengazo. Mlembi Ezara adaaimirira pa nsanja yamitengo, imene anthuwo adaamanga chifukwa cha msonkhanowo. Ku dzanja lake lamanja kudaaimirira Matitiya, Sema, Anaya, Uriya, Hilikiya ndi Maaseiya. Ku dzanja lake lamanzere kudaaimirira Pedaya, Misaele, Malikiya, Hasumu, Hasibadana, Zekariya ndiponso Mesulamu. Tsono ataimirira pansanjapo, Ezara adafutukula buku, anthu onse akupenya. Pomwepo anthu onse adaimirira. Kenaka Ezara adati, “Atamandike Chauta, Mulungu wamkulu!” Ndipo anthu onse adakweza manja nayankha kuti, “Inde momwemo, inde momwemo.” Pambuyo pake adaŵeramitsa mitu pansi ndipo adapembedza Chauta ali chizyolikire. Anthu ataimiriranso, Alevi adaŵathandiza kuti amvetse malamulo. Aleviwo anali aŵa: Yesuwa, Bani, Serebiya, Yamini, Akubu, Sabetai, Hodiya, Maaseiya, Kelita, Azariya, Yozabadi, Hanani ndiponso Pelaya. Aleviwo adaŵerenga buku la Malamulo a Mulungu momveka bwino, ndipo adatanthauzira mauwo kuti anthu amvetse bwino. Tsono bwanamkubwa Nehemiya, pamodzi ndi Ezara wansembe ndi mphunzitsi wa malamulo, kudzanso Alevi amene ankaphunzitsa anthu, adauza anthu onse aja kuti, “Lero ndi tsiku loyera kwa Chauta, Mulungu wanu. Musakhale ndi chisoni ndipo musalire.” Ndiye kuti anthu onse ankalira atamva mau a Malamulowo. Tsono Nehemiya adapitiriza nati, “Kazipitani, mukachite phwando ku nyumba, kenaka muŵapatseko anzanu amene sadakonze kanthu. Pakuti lero ndi tsiku loyera kwa Chauta, Mulungu wathu. Tsono musakhale ndi chisoni, popeza kuti chimwemwe chimene Chauta amakupatsani, chimakulimbikitsani.” Choncho Alevi adacheteketsa anthu onse naŵauza kuti, “Musalirenso ai, pakuti lero ndi tsiku loyera, choncho musakhale ndi chisoni.” Pamenepo anthu onse adapita kwao kukadya ndi kumwa ndipo zakudya zina adagaŵirako anzao, kuti pakhale chikondwerero chachikulu, chifukwa chakuti tsopano anali atamvetsa bwino mau a Malamulo amene adaaŵerengedwawo. Atsogoleri a mabanja, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi, onse adabwera m'maŵa mwake kwa Ezara, mphunzitsi wa malamulo, kuti aphunzire mau a Malamulowo. Tsono adapeza kuti m'buku la Malamulo mudalembedwa kuti Chauta adalamula kudzera mwa Mose kuti Aisraele azikhala m'zithando nthaŵi yonse ya chikondwerero cha pa mwezi wachisanu ndi chiŵiri. Motero adafalitsa ndi kulengeza m'midzi yao yonse ndiponso m'Yerusalemu, kuti, “Pitani ku mapiri, mukatengeko nthambi za mtengo wa olivi, za mtengo wa olivi wakuthengo, za mtengo wa mchisu, za mtengo wa mgwalangwa, ndiponso za mitengo ina ya masamba ambiri, kuti mumangire misasa monga momwe zidalembedwera.” Choncho anthuwo adapita nakatenga zonsezo ndipo aliyense adadzimangira misasa padenga pa nyumba yake, ndiponso m'mabwalo ao, m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu, m'bwalo la pa Chipata cha Madzi ndi m'bwalo la pa Chipata cha Efuremu. Motero onse amene adaasonkhana, ndiye kuti amene adaabwerako ku ukapolo, adamanga misasa, ndipo adakhala m'menemo. Kuyambira nthaŵi ya Yoswa, mwana wa Nuni, mpaka tsiku limenelo, Aisraele anali asanachitepo zoterozo. Motero kunali chikondwerero chachikulu kwambiri. Tsiku ndi tsiku kuyambira tsiku loyamba mpaka tsiku lotsiriza, Ezara ankaŵerenga buku la Malamulo a Mulungu. Anthu adachita chikondwerero masiku asanu ndi aŵiri, ndipo pa tsiku lachisanu ndi chitatu padachitika mwambo wotseka msonkhano, potsata buku la Malamulo lija. Tsono tsiku la 24 la mwezi womwewo, Aisraele onse adasonkhana kuti asale chakudya, kuvala chiguduli ndi kudzithira dothi pa mutu. Aisraele atadzipatula pakati pa anthu a mitundu ina, adaimirira, nayamba kuulula machimo ao ndi zolakwa za makolo ao. Anthuwo adaimirira pomwepo, ndipo adamva mau a m'buku la Malamulo a Chauta akuŵaŵerenga nthaŵi yokwanira maora atatu. Pa maora atatu enanso, anthuwo ankaulula machimo ao namapembedza Chauta, Mulungu wao. Pa makwerero okhalapo Alevi padaimirira Yesuwa, Bani, Kadimiyele, Sebaniya, Buni, Serebiya, Bani ndi Kenani. Onsewo ankapemphera mokweza mau kwa Chauta, Mulungu wao. Tsono Alevi aŵa, Yesuwa, Kadimiyele, Bani, Hasabeniya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya ndi Petahiya adalengeza kuti, “Imirirani, mumtamande Chauta, Mulungu wanu, nthaŵi zonse. Litamandike dzina lake laulemerero limene anthu sangathe kulilemekeza ndi kulitamanda mokwanira.” Pamenepo Ezara adapemphera kuti, “Inu nokha ndiye Chauta. Inu mudalenga kumwamba, kumwambamwamba, ndiponso zonse zokhala komweko, dziko lapansi ndi zonse zokhala m'menemo. Mudalenga nyanja ndi zonse zam'menemo. Zonse zakumwamba zimakupembedzani. Inu ndinu Chauta, Mulungu amene mudasankha Abramu, kumtulutsa ku Uri wa ku Kaldeya, ndi kumutcha dzina loti Abrahamu. Mudaona kuti mtima wake unali wokhulupirika kwa Inu, ndipo mudachita naye chipangano chakuti zidzukulu zake mudzazipatsa dziko la Akanani, la Ahiti, la Aamori, la Aperezi, la Ayebusi ndi la Agirigasi. Mudachitadi zimene mudalonjezazo, pakuti Inu ndinu olungama. “Mudaona kuzunzika kwa makolo athu ku Ejipito kuja, ndipo mudamva kulira kwao ku Nyanja Yofiira. Mudachita zizindikiro ndi zodabwitsa pamaso pa Farao, antchito ake onse, ndi anthu onse okhala m'dziko mwake, popeza kuti mudaadziŵa kuti iwowo adazunza makolo athu. Nchifukwa chake mbiri yanu idakula monga momwe iliri mpaka lero lino. Mudagaŵa nyanja pakati, anthu anu akupenya, kotero kuti iwowo adaoloka pakati pa nyanja pali pouma. Kenaka mudaŵamiza m'nyanja adani amene ankaŵalondola, monga momwe umachitira mwala m'madzi ozama. Munkaŵatsogolera masana ndi mtambo, ndipo usiku munkaŵaunikira ndi moto njira imene ankayendamo. Mudatsika pa phiri la Sinai, ndipo mudalankhula nawo kuchokera kumwamba. Mudaŵapatsa malangizo olungama, malamulo oona, zophunzitsa zabwino ndiponso mau aluntha. Mudaŵadziŵitsa kuti tsiku lanu la Sabata ndi lopatulika, ndipo mudaŵapatsa malamulo, malangizo, ndiponso mau anu, kudzera mwa Mose mtumiki wanu. Mudaŵapatsa buledi wochokera kumwamba kuti adye. Mudaŵapatsa madzi otuluka m'thanthwe, kuti aphere ludzu. Mudaŵauza kuti apite kukalanda dziko limene Inu mudaalonjeza kuti mudzaŵapatsa. “Koma makolo athu adadzitukumula nakhala okanika ndipo sadamvere malamulo anu. Adakana kumvera, ndipo sankakumbuka zodabwitsa zimene Inu mudaazichita pakati pao. Adakhala okanika, nadzisankhira mtsogoleri woti aŵatsogolere kubwerera ku Ejipito ku dziko laukapolo lija. Koma Inu ndinu Mulungu wokhululuka, wokoma mtima, wachifundo, wosakwiya msanga, wokhala ndi chikondi chachikulu chosasinthika, motero iwowo simudaŵasiye. Ngakhale pamene adadzipangira fano la mwanawang'ombe, namanena kuti, ‘Uyu ndiye Mulungu wathu amene adatitulutsa ku dziko la Ejipito,’ ndipo ngakhale adachita zinthu zoipitsitsa zokunyozani, Inu amene muli ndi chifundo chachikulu, simudaŵasiye m'chipululu iwowo. Mtambo umene unkaŵatsogolera poyenda m'njira masana sudaŵachokere, ndipo moto umene unkaŵaunikira njira poyenda usiku sudaŵasiye. Inu mudaŵapatsa mzimu wanu wabwino kuti aziŵalangiza. Simudaŵamane chakudya cha mana chija, ndipo mudaŵapatsa madzi akumwa, kuti aphe ludzu lao. Mudaŵasunga zaka makumi anai m'chipululu ndipo nthaŵi yonseyo sankasoŵa kanthu. Zovala zao sizidathe, mapazi aonso sadatupe. Mudaŵapatsa mphamvu zogonjetsera maiko ndiponso mitundu ya anthu. Mudaŵagaŵiranso maiko achilendo, ndipo choncho adalanda dziko la Sihoni mfumu ya ku Hesiboni, ndi dziko la Ogi mfumu ya ku Basani. Mudachulukitsa zidzukulu zao ngati nyenyezi zamumlengalenga. Mudaŵaloŵetsa m'dziko limene mudaauza makolo ao kuti adzalilandira nkukhala lao. Choncho zidzukulu zaozo zidaloŵamo ndi kukhazikika m'menemo, ndipo Inu mukuŵatsogolera, mudagonjetsa Akanani, nzika za m'dzikomo. Akananiwo, ndiye kuti mafumu ao ndi anthu onse am'dzikomo, mudaŵapereka kwa anthu anu, kuti achite nawo monga angafunire. Motero adagonjetsa mizinda yamalinga nalanda dziko lachonde, nyumba zodzaza ndi zinthu zabwino, zitsime zokumbakumba, minda yamphesa, minda yaolivi ndiponso mitengo yazipatso yochuluka kwambiri. Choncho iwowo ankadya, namakhuta, mpaka kumanenepa, ndipo ankakondwa chifukwa cha ubwino wanu, Inu Chauta. “Komabe iwowo sankamvera, ndipo adakuukirani. Adaŵataya kunkhongo Malamulo anu, napha aneneri anu amene ankaŵadzudzula kuti abwerere kwa Inu. Adachita zinthu zoipitsitsa zokunyozani. Nchifukwa chake Inu mudaŵapereka kwa adani ao amene ankaŵavuta. Pa nthaŵi imene anali m'mavutoyo, ankalira kwa Inu, ndipo Inu munkaŵamvera muli Kumwambako. Chifukwa cha chifundo chanu chachikulu, mudaŵapatsa atsogoleri amene ankaŵapulumutsa kwa adani ao. Koma atakhala pa mtendere, adayambanso kuchimwa pamaso panu, ndipo mudaŵaperekanso kwa adani ao, kotero kuti adani aowo ankaŵalamulira. Komabe pamene ankabwerera ndi kumalira Inu, Inuyo munkaŵamvera muli Kumwambako. Motero nthaŵi zambiri munkaŵapulumutsa chifukwa cha chifundo chanu. Zoonadi Inu mudaŵachenjeza kuti ayambenso kutsata Malamulo anu. Koma iwo ankadzitukumula, ndipo sankamvera malamulo anu. Adachimwira malangizo anu opatsa moyo kwa anthu oŵasunga. Ankakufulatirani namaumitsa mitu yao, osafuna kumvera. Mudaŵapirira zaka zambiri ndipo munkaŵachenjeza ndi mzimu wanu kudzera mwa aneneri anu, komabe sadafune kutchera khutu. Nchifukwa chake mudaŵapereka kwa anthu a m'maiko ena. Ngakhale zinali choncho, Inu simudaŵaononge kotheratu, kapena kuŵasiya, pakuti Inu ndinu Mulungu wokoma mtima ndi wachifundo. “Nchifukwa chake tsono, Inu Mulungu wathu, Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi woopsa, mumasunga chipangano ndi chikondi chanu chosasinthika. Musalole kuti zosautsa zathu zonse zikuwonekereni ngati zochepa. Zosautsazo zatigwera ife, mafumu athu, akulu athu, ansembe athu, aneneri athu, makolo athu, ndiponso anthu anu onse, kuyambira nthaŵi ya mafumu a ku Asiriya mpaka lero lino. Komabe Inu mwakhala olungama pa zonse zimene zatigwera, ndipo mwachita zokhulupirika, koma ife tachita zolakwa. Mafumu athu, akulu athu, ansembe athu ndi makolo athu, sadasunge mau anu, ndipo sadasamale malamulo anu ndi malangizo anu amene mudaŵapatsa. Pamene iwo ankadzilamulira okha, namalandira zabwino zanu m'dziko lalikulu ndi lachonde limene mudaŵapatsa, sadakutumikireni, ndipo sadazisiye ntchito zao zoipa. Onani, ife ndife akapolo lero lino, ndife akapolo m'dziko limene mudapatsa makolo athu, kuti azidya zipatso zake ndi zabwino zake zonse. Tsopano chuma cha dzikolo changolemeza mafumu amene mudaŵaika kuti azitilamulira kaamba ka machimo athu. Ali ndi mphamvu zolamulira matupi athu ndiponso ng'ombe zathu monga afunira. Ndithudi, ife tili m'mavuto aakulu.” Chifukwa cha zonsezi tikuchita chipangano chotsimikizika chichita kulemba, ndipo akuluakulu athu, Alevi athu ndi ansembe athu asindikiza chidindo pa chipanganocho. Anthu amene adasindikiza chidindo chao movomereza chipanganocho ndi aŵa: Nehemiya, bwanamkubwa uja, mwana wa Hakaliya, Zedekiya, Senaya, Azariya, Yeremiya, Pasuri, Amariya, Malakiya, Hatusi, Sebaniya, Maluki, Harimu, Meremoti, Obadiya, Daniele, Ginetoni, Baruki, Mesulamu, Abiya, Miyamini, Maziya, Biligai ndi Semaya. Ameneŵa ndiwo anali ansembe. Alevi anali aŵa: Yesuwa mwana wa Azaniya, Binuyi, wa fuko la Henadadi, Kadimiyele, ndi abale ao aŵa: Sebaniya, Hodiya, Kelita, Pelaya, Hanani, Mika, Rehobu, Hasabiya, Zakuri, Serebiya, Sebaniya, Hodiya, Bani ndi Benimu. Atsogoleri a anthu anali aŵa: Parosi, Pahatimowabu, Elamu, Zatu, Bani, Buni, Azigadi, Bebai, Adoniya, Bigivai, Adini, Atere, Hezekiya, Azuri, Hodiya, Hasumu, Bezai, Harifi, Anatoti, Nebai, Magapiyasi, Mesulamu, Heziri, Mesezabele, Zadoki, Yaduwa, Pelatiya, Hanani, Anaiya, Hoseya, Hananiya, Hasubu, Halohesi, Piliha, Sobeki, Rehumu, Hasabuna, Maaseiya, Ahiya, Hanani, Anani, Maluki, Harimu ndi Baana. Ife otsalafe, ansembe, Alevi, alonda a pa Nyumba ya Mulungu, oimba nyimbo, atumiki a ku Nyumba ya Mulungu, ndi onse amene ankadzipatula kwa mitundu ina ya anthu ya m'maiko achilendo, kuti atsate Malamulo a Mulungu, tonse, pamodzi ndi akazi athu, ana athu ndi onse amene ali ndi nzeru zokwanira, tikuphatikana ndi abale athu olemekezeka, ndipo tikulonjeza molumbira kuti tidzayenda motsata Malamulo a Mulungu amene adaŵapereka Mose mtumiki wa Mulungu. Tidzamvera ndi kuchitadi zimene Malamulo a Chauta, Mulungu wathu, amanena. Tidzamveranso malangizo ndi miyambo yake yolamulidwa. Ndipo titembereredwe tikalephera kuchita zimenezi. Sitidzapereka ana athu aakazi kuti akakwatiwe ndi anthu a mitundu ina ya m'dzikomo, sitidzalolanso ana athu aamuna kuti akakwatire ana ao aakazi. Ndipo ngati anthu a mitundu ina ya m'dzikomo abwera ndi zinthu zamalonda kapena tirigu, kudzagulitsa pa tsiku la sabata, sitidzaŵagula pa tsiku limenelo, kapenanso pa tsiku loyera lina lililonse. Pa chaka chilichonse chachisanu ndi chiŵiri, tidzagoneka munda osaulima, ndipo tidzafafaniza ngongole zonse. Tikulumbiranso kuti chaka ndi chaka tizipereka magaramu anai a siliva, kuti tithandize pa ntchito za ku Nyumba ya Mulungu wathu. Tiziperekanso ndalama zolipirira buledi woperekedwa, chopereka cha chakudya ndiponso nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku, zopereka za pa masabata, za pokhala mwezi, za pa masiku achikondwerero osankhidwa, zoperekera zinthu zopatulika ndiponso nsembe zopepesera machimo a Aisraele, kudzanso zoperekera china chilichonse chofunika pa ntchito ya ku Nyumba ya Mulungu. Ife ansembe, Alevi ndi anthu wamba tidzachita maele, kuti tisankhe mabanja amene adzapereke nkhuni ndi kubwera nazo ku Nyumba ya Mulungu wathu, pa nthaŵi zake zoikidwa, chaka ndi chaka, kuti azipserezera nsembe za pa guwa la Chauta, Mulungu wathu, monga mudalembedwera m'Malamulo. Tikulonjezanso kuti tidzabwera ndi zipatso zoyamba kucha za kuminda kwathu, ndi zipatso zoyamba kucha za mtengo uliwonse wazipatso, chaka ndi chaka, kuti tizipereke ku Nyumba ya Chauta. Tidzaperekanso kwa Mulungu ana athu aamuna oyamba kubadwa. Ana a ng'ombe oyamba kubadwa ndiponso ana oyamba kubadwa a nkhosa ndi a mbuzi zathu, tidzapereka kwa ansembe amene amatumikira ku Nyumba ya Mulungu, monga mudalembedwera m'Malamulo. Ndipo ku zipinda za Nyumba ya Mulungu wathu, tidzaperekanso kwa ansembewo mtanda wathu wa buledi wa ufa woyamba, ndiponso mphatso zathu zina, monga zipatso za mtengo uliwonse, vinyo ndi mafuta. Tidzaperekanso kwa Alevi chimodzi mwa zigawo khumi za zinthu za m'minda mwathu, pakuti Alevi ndiwo amene amasonkhanitsa zigawo zonse zachikhumi m'midzi yathu yonse. Wansembe, mdzukulu wa Aroni, adzakhale pamodzi ndi Alevi, pamene Aleviwo akulandira zigawo zachikhumizo. Ndipo Alevi adzabwera ndi zigawozo ku Nyumba ya Mulungu wathu, ku zipinda zosungiramo katundu. Aisraele ndiponso a m'banja la Levi adzapereka tirigu, vinyo ndi mafuta kuzipinda kosungira ziŵiya za m'malo opatulika, ndiponso kokhala ansembe amene akutumikira, pamodzi ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu, ndi anthu oimba nyimbo. Ndithu ife tidzasamala Nyumba ya Mulungu wathu. Nthaŵi imeneyo atsogoleri a mabanja a Aisraele ankakhala ku Yerusalemu. Tsono anthu ena onse adachita maele kuti apeze munthu mmodzi pa anthu khumi aliwonse oti azikhala ku Yerusalemu, mzinda wopatulikawo, ndipo anthu asanu ndi anai otsala azikhalabe m'midzi. Ndipo anthu adayamika anzao onse amene adadzipereka kuti azikhala ku Yerusalemu. Aisraele wamba ambiri, pamodzi ndi ansembe, Alevi, anthu otumikira ku Nyumba ya Mulungu, ndiponso zidzukulu za atumiki a Solomoni, onsewo ankakhala m'midzi mwao, aliyense m'dera la choloŵa chake. Koma akuluakulu a m'chigawo cha Yuda anali atakhazikika ku Yerusalemu. Ku Yerusalemu kunkakhalanso ena a fuko la Yuda ndiponso ena a fuko la Benjamini. Zina mwa zidzukulu za Yuda ndi izi: Ataya mwana wa Uziya, mwana wa Zekariya, mwana wa Amariya, mwana wa Sefatiya, mwana wa Mahalalele, onsewo anali ana a Perezi. Panalinso Maaseiya mwana wa Baruki, mwana wa Kolihoze, mwana wa Hazaya, mwana wa Adaya, mwana wa Yoyaribu, mwana wa Zekariya, mwana wa Msiloni. Ana ndi adzukulu onse a Perezi amene ankakhala ku Yerusalemu analipo anthu akuluakulu okwanira 468. Zidzukulu za Benjamini zinali izi: Salu mwana wa Mesulamu, mwana wa Yoedi, mwana wa Pedaya, mwana wa Kolaya, mwana wa Maaseiya, mwana wa Itiyele, mwana wa Yesaya. Achibale ake anali Gabai ndi Salai. Onse pamodzi analipo 928. Yowele, mwana wa Zikiri, ndiye amene anali kapitao wao. Ndipo Yuda mwana wa Hasenuwa anali kapitao wachiŵiri wa mumzindamo. Ansembe anali aŵa: Yedaya mwana wa Yoyaribu, Yakini, Seraya mwana wa Hilikiya, mwana wa Mesulamu, mwana wa Zadoki, mwana wa Meraiyoti, mwana wa Ahitubi amene anali mkulu wa ansembe ku Nyumba ya Mulungu, ndiponso achibale ao amene ankagwira ntchito m'Nyumbamo, onse pamodzi analipo 822. Panalinso Adaya, mwana wa Yerohamu, mwana wa Pelaliya, mwana wa Amizi, mwana wa Zekariya, mwana wa Pasuri, mwana wa Malikiya ndiponso achibale ao amene anali akuluakulu a banja lao. Onse pamodzi analipo 242. Amasisai, mwana wa Azarele, mwana wa Ahazai, mwana wa Mesilemoti, mwana wa Imeri, ndiponso achibale ao amene anali ankhondo olimba mtima. Onse pamodzi analipo 128, ndipo kapitao wao anali Zabidiele, mwana wa Hagedolimu. Alevi anali aŵa: Semaya, mwana wa Hasubu, mwana wa Azirikamu, mwana wa Hasabiya, mwana wa Buni. Sabetai ndiponso Yozabadi anali atsogoleri a Alevi amene ankayang'anira ntchito ya kunja kwa Nyumba ya Mulungu. Mataniyo, mwana wa Mika, mwana wa Zabidi, mwana wa Asafu, amene anali mtsogoleri pa mapemphero achiyamiko m'Nyumba ya Mulungu, ndiponso Bakibukiya, amene anali wachiŵiri pakati pa abale ake. Panalinso Abida, mwana wa Samuwa, mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni. Alevi onse amene ankakhala mu mzinda wopatulika analipo 284 pamodzi. Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali aŵa: Akubu, Talimoni ndiponso achibale ao onse pamodzi analipo 172. Aisraele ena ndiponso ansembe ndi Alevi otsala anali m'midzi ya Yuda ndipo aliyense ankakhala m'dera la choloŵa chake. Koma anthu otumikira ku Nyumba ya Mulungu ankakhala ku Ofele, mu Yerusalemu, ndipo Ziha ndi Gisipa ankaŵayang'anira. Kapitao wa Alevi ku Yerusalemu anali Uzi, mwana wa Bani, mwana wa Hasabiya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mika. Anali mmodzi mwa zidzukulu za a Asafu, amene anali oimba nyimbo zofunika pa miyambo ya m'Nyumba ya Mulungu. Pakuti mfumu idaalamula kuti magulu oimbawo azikhalapo tsiku ndi tsiku, potsogolera maimbidwe a nyimbo za m'Nyumba ya Mulungu. Tsono Petahiya, mwana wa Mesezabele, mmodzi mwa adzukulu a Sera wa m'fuko la Yuda, ankaimirira Aisraele ku bwalo la mfumu ya ku Persiya. Anthu ena a fuko la Yuda ankakhala ku Kiriyati-Ariba ndi midzi yake, ku Diboni ndi midzi yake, ku Yekabizeele ndi midzi yake. Ankakhalanso ku Yesuwa, ku Molada ndi ku Betepeleti, ku Hazarisuwala, ku Beereseba ndi midzi yake. Ena ankakhala ku Zikilagi, ku Mekona ndi midzi yake, ku Enirimoni, ku Zora, ku Yarimuti, Zanowa, Adulamu ndi midzi yake. Ankakhalanso ku Lakisi ndi ku minda yake, ku Azeka ndi midzi yake. Motero ankakhala m'midzi yonse kuyambira ku Beereseba mpaka ku chigwa cha Hinomu. Anthu a fuko la Benjamini nawonso adakhala kuyambira ku Geba, kubzola mpaka ku Mikimasi, Aiya, Betele ndi midzi yake, Anatoti, Nobi, Ananiya, Hazori, Rama, Gitaimu, Hadidi, Zeboimu, Nebalati, Lodi, Ono, ndiponso ku chigwa cha anthu aluso. Magulu ena a Alevi amene ankakhala m'dziko la Yuda adasamukira ku dziko la Benjamini. Ansembe ndi Alevi, amene adabwerera pamodzi ndi Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndiponso ndi Yesuwa, anali aŵa: Seraya, Yeremiya, Ezara, Amariya, Maluki, Hatusi, Sekaniya, Rehumu, Meremoti, Ido, Ginetoyi, Abiya, Miyamini, Maadiya, Biliga, Semaya, Yoyaribu, Yedaya, Salu, Amoki, Hilikiya, ndi Yedaya. Ameneŵa anali atsogoleri pakati pa ansembe ndi achibale ao pa nthaŵi ya Yesuwa. Alevi anali aŵa: Yesuwa, Binuyi, Kadimiyele, Serebiya ndi Yuda. Panalinso Mataniya, amene ankayang'anira za maimbidwe a nyimbo zachiyamiko, pamodzi ndi anzakewo. Abale ao, Bakibukiya ndi Uni, ankaimba molandizana nawo pa nthaŵi ya chipembedzo. Yesuwa adabereka Yoyakimu, Yoyakimu adabereka Eliyasibu, Eliyasibu adabereka Yoyada, Yoyada adabereka Yonatani ndipo Yonatani adabereka Yaduwa. Pa nthaŵi ya Yoyakimu, mkulu wa ansembe, atsogoleri a mabanja a ansembe anali aŵa: Mtsogoleri wa fuko la Seraya anali Meraya. Wa fuko la Yeremiya, anali Hananiya. Wa fuko la Ezara anali Mesulamu, wa fuko la Amariya anali Yehohanani. Wa fuko la Maluki anali Yonatani, wa fuko la Sebaniya anali Yosefe. Wa fuko la Harimu anali Adina, wa fuko la Meraiyoti anali Helikai. Wa fuko la Ido anali Zekariya, wa fuko la Ginetoni anali Mesulamu. Wa fuko la Abiya anali Zikiri, wa fuko la Miniyamini, wa fuko la Mowadiya anali Pilitai. Wa fuko la Biliga anali Samuwa, wa fuko la Semaya anali Yehonatani. Wa fuko la Yoyaribu anali Matenai, wa fuko la Yedaya anali Uzi. Wa fuko la Salai anali Kalai, wa fuko la Amoki anali Eberi. Wa fuko la Hilikiya anali Hasabiya ndipo wa fuko la Yedaya anali Netanele. Pa nthaŵi ya Eliyasibu, Yoyada, Yohanani ndi Yaduwa, amene anali akulu a ansembe, padalembedwa maina a atsogoleri a mabanja a Alevi ndi a ansembe, mpaka pa nthaŵi imene mfumu Dariusi wa ku Persiya ankalamulira. Adzukulu a Levi, makamaka atsogoleri a mabanja ao, adalembedwa m'buku la Mbiri, mpaka pa nthaŵi ya Yohanani mwana wa Eliyasibu. Atsogoleri a Alevi, Hasabiya, Serebiya ndi Yesuwa mwana wa Kadimiyele, ankathandizana ndi abale ao poimba nyimbo zotamanda ndi zothokoza, monga momwe Davide, munthu wa Mulungu, adaaŵalamulira kuti gulu liziimba molandizana ndi gulu linzake. Mataniya, Bakibukiya, Obadiya, Mesulamu, Talimoni ndi Akubu, anali olonda nyumba zosungiramo chuma pa zipata za ku Nyumba ya Mulungu. Ameneŵa ndiwo adaalipo pa nthaŵi ya Yoyakimu mwana wa Yesuwa, mwana wa Yozadaki, ndiponso pa nthaŵi ya bwanamkubwa Nehemiya ndi wansembe Ezara amene analinso katswiri wa malamulo. Pamene anthu adati apereke kwa Mulungu khoma lozinga mzinda wa Yerusalemu, adaitana Alevi kuchokera konse kumene ankakhala, kuti abwere ku Yerusalemu kudzachita mwambo wopereka khomalo mokondwera, mothokoza ndiponso poimba pamodzi ndi ziwaya zamalipenga, azeze ndi mapangwe. Tsono anthu a m'mabanja a Levi oimba nyimbo, adasonkhana pamodzi, kuchokera ku malo onse ozungulira Yerusalemu, ndiponso ku midzi ya Anetofati. Kudabwera enanso ochokera ku Betegiligala, ku Geba, ndi ku Azimaveti, pakuti oimba nyimbo anali atamanga midzi yao pozungulira Yerusalemu. Tsono ansembe ndi Alevi adachita mwambo wa kudziyeretsa. Mwambowu adachitiranso anthu, ndiponso zipata ndi khoma la mzinda. Ineyo ndidadza nawo akuluakulu a ku dziko la Yuda ndipo ndidakwera nawo pa khoma. Ndidasankha magulu aŵiri mwa iwo, kuti aziyenda mu mdipiti ndi kumathokoza Mulungu. Mdipiti wina unkadzera cha ku dzanja lamanja pa khoma mpaka kukafika ku Chipata cha Kudzala. Pambuyo pao pankadza Hosaya ndi theka la akuluakulu aja, ndiponso Azariya, Ezara, Mesulamu, Yuda, Benjamini, Semaya ndi Yeremiya. Ena mwa ana a ansembe amene ankaimba malipenga anali aŵa: Zekariya mwana wa Yonatani, mwana wa Semaya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mikaya, mwana wa Zakuri, mwana wa Asafu. Panali achibale ao aŵa: Semaya, Azarele, Milalai, Gilalai, Maai, Netanele, Yuda, ndi Hanani. Iwowo ankanyamula zoimbira zopangidwa ndi Davide, munthu wa Mulungu uja. Mlembi Ezara ndiye ankaŵatsogolera. Kuchokera ku Chipata cha Kasupe, adakwera pa makwerero opita ku mzinda wa Davide, pa njira yotsatira khoma, chakumtunda kwa nyumba ya Davide, mpaka kukafika ku Chipata cha Madzi, kuvuma kwa mzinda wa Yerusalemu. Mdipiti wina wa anthu othokoza Mulungu udadzera chakumanzere kwa khomalo, ndipo ine ndidautsata pambuyo, poyenda pa khoma pamodzi ndi theka lina la akuluakulu. Tidapitirira Nsanja ya Ng'anjo, kukafika ku Khoma Lotambasuka. Tidadzeranso pa Chipata cha Efuremu, pa Chipata Chakale, pa Chipata cha Nsomba, pa Nsanja ya Hananele, pa Nsanja ya Zana, mpaka kukafika ku Chipata cha Nkhosa. Ndipo potsiriza tidakaima ku Chipata cha Mlonda. Choncho magulu othokoza aŵiri onsewo adakaimirira pafupi ndi Nyumba ya Mulungu. Pamodzi ndi ine ndi theka la akuluakulu aja, panali ansembe aŵa akuimba malipenga: Eliyakimu, Maaseiya, Miniyamini, Mikaya, Eliyoenai, Zekariya ndi Hananiya. Panalinso ansembe aŵa: Maaseiya, Semaya, Eleazara, Uzi, Yehohanani, Malikiya, Elamu ndi Ezero. Yezeraya ndiye ankatsogolera oimba nyimbo. Pa tsiku limenelo anthu adapereka nsembe zochuluka, ndipo adakondwa kwakukulu, popeza kuti Mulungu ndiye adaŵakondwetsa. Akazi nawonso, pamodzi ndi ana, adakondwa, ndipo kukondwa kwa anthu a ku Yerusalemu kudamveka patali. Tsiku limenelo padasankhidwa anthu oyang'anira zipinda zosungiramo zopereka zaufulu, zipatso zoyamba kucha, ndi zopereka zachikhumi. Anthuwo ankasonkhanitsa zopereka potsata Malamulo a Mose, kuti azipereka kwa ansembe ndi Alevi, kuchokera ku minda ya midzi yonse. Pakuti Ayuda ankakondwera nawo ansembe ndi Alevi otumikirawo, chifukwa ankachita zimene Mulungu wao adaalamula, makamaka mwambo wopatulira zinthu. Oimba nyimbo ndiponso alonda a ku Nyumba ya Mulungu nawonso ankagwira ntchito zao potsata lamulo la Davide ndi Solomoni mwana wake. Pa nthaŵi ya Davide ndi Asafu, panali mtsogoleri wa anthu oimba nyimbo, ndiponso panali nyimbo zotamanda ndi zothokoza Mulungu. Pa nthaŵi ya Zerubabele ndi Nehemiya, anthu a m'dziko lonse la Israele ankapereka tsiku ndi tsiku mphatso zofunika kwa anthu oimba nyimbo ndiponso kwa alonda a ku Nyumba ya Mulungu. Ankaikanso padera chigawo cha Alevi, ndipo Aleviwo nawonso ankaika padera chigawo cha ansembe, adzukulu a Aroni. Pa tsiku limenelo adaŵerenga buku la Mose, anthu onse alikumva. Ndipo adafika pa mau akuti, “Mwamoni kapena Mmowabu asaloŵe konse mu msonkhano wa Mulungu. Paja ameneŵa sadapite kukakomana ndi ana a Aisraele, kuti akaŵapatse buledi ndi madzi. M'malo mwake adalemba Balamu kuti aŵatemberere. Komabe Mulungu wathu matembererowo adaŵasandutsa madalitso.” Tsono pamene anthuwo adamva lamulolo, adachotsa anthu onse achilendo pakati pa gulu lao. Koma zimenezi zisanachitike, wansembe Eliyasibu anali atasankhidwa kuti aziyang'anira zipinda zosungira katundu m'Nyumba ya Mulungu. Chifukwa chomvana ndi Tobiya, iyeyo adakonzera Tobiyayo chipinda chachikulu m'mene kale ankasungiramo zopereka zaufa, lubani, ziŵiya, mphatso zoyenerera ansembe, ndiponso zopereka za chachikhumi cha chakudya, vinyo ndi mafuta, zimene adaalamula kuti azipatse Alevi, anthu oimba nyimbo ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu, potsata malamulo a Mose. Pamene zimenezi zinkachitika ku Yerusalemu, nkuti ine palibe, popeza kuti pa chaka cha 32 cha ufumu wa Arita-kisereksesi, mfumu ya ku Babiloni, ine ndidaapita kwa mfumuyo. Patapita nthaŵi ndithu, ndidapempha chilolezo kwa mfumu, ndipo ndidabwereranso ku Yerusalemu. Tsono ndidapeza cholakwa chimene Eliyasibu adaachita pomkonzera Tobiya chipinda m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu. Pamenepo ndidapsa mtima kwambiri, ndipo ndidamtaya kunja katundu yense wa Tobiya amene anali m'chipindamo. Tsono ndidalamula kuti ayeretse zipindazo. Kenaka ndidabwezeranso ziŵiya za m'Nyumba ya Mulungu, pamodzi ndi zopereka za chakudya ndi lubani. Ndidapezanso kuti Alevi sankaŵapatsa magawo ao amene ankayenera kulandira. Choncho Aleviwo, pamodzi ndi anthu oimba nyimbo amene ankagwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu, adathaŵa, aliyense kupita ku munda wake. Choncho ndidaŵadzudzula akuluakulu aja kuti, “Kodi chifukwa chiyani Nyumba ya Mulungu yasiyidwa chonchi?” Ndipo ndidasonkhanitsa anthu aja ndi kuŵaikanso pa ntchito zimene ankazigwira Nditachita zimenezi, Ayuda adayambanso kubwera ndi zopereka za chachikhumi cha tirigu, vinyo ndi mafuta, kuti azipereka ku nyumba zosungira chuma. Ndipo ndidasankha aŵa kuti akhale asungachuma: wansembe Selemiya, mlembi Zadoki ndiponso Pedaya mmodzi mwa Alevi, kudzanso mthandizi wao Hanani, mwana wa Zakuri, mdzukulu wa Mataniya, popeza kuti ndidaadziŵa kuti anthuwo anali okhulupirika. Ntchito yao inali yogaŵira abale ao zinthu zofunika. Inu Mulungu wanga, mundikumbukire ine pa zimenezi. Musaiŵale ntchito zanga zabwino zimene ndachitira Nyumba ya Mulungu wanga pofuna kumtumikira. Nthaŵi imeneyo ndidaona anthu m'dziko la Yuda akuponda ndi kufinya mphesa pa tsiku la sabata. Ena ankaunjika tirigu milumilu, nkumasenzetsa abulu. Enanso ankatenga vinyo, mphesa, nkhuyu, ndiponso katundu wa mtundu uliwonse, nkumabwera naye ku Yerusalemu, pa tsiku la sabata. Tsono ndidaŵachenjeza kuti asamagulitse chakudya pa tsiku la sabata. Nawonso anthu ena a ku Tiro okhala mu Yerusalemu, ankabwera ndi nsomba ndi zamalonda za mtundu uliwonse, nkumazigulitsa pa tsiku la sabata kwa anthu a m'dziko la Yuda ndiponso kwa anthu okhala mu mzinda wa Yerusalemu. Pomwepo ndidadzudzula atsogoleri a Ayuda, ndipo ndidaŵafunsa kuti, “Monga simukuzindikira choipa chimene mukuchitachi pakuipitsa tsiku la sabata chonchi? Makolo anu adachitanso motero momwemu, ndipo Mulungu wathu adadzetsa chiwonongeko pa ife ndi pa mzinda uno. Koma inu mukufuna kuutsanso mkwiyo wa Chauta pa Aisraele, pamene mukuipitsa tsiku la sabata motere.” Nchifukwa chake ndikulamula kuti pamene kuziyamba kuda, tsiku la sabata lisanayambike, azitseka zipata zonse za Yerusalemu, ndipo asazitsekule mpaka tsiku la sabata litapita. Ndidaika antchito anga ena oyang'anira pa zipata, kuti katundu aliyense asaloŵe mumzindamo pa tsiku la sabata. Motero anthu amalonda ogulitsa zinthu zamitundumitundu ankagona kunja kwa mzinda wa Yerusalemu kamodzi kapena kaŵiri konse. Koma ndidaŵachenjeza ndipo ndidaŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukugona pafupi ndi khoma? Mukachitanso zimenezi ndidzakumangani.” Kuyambira nthaŵi imeneyo mpaka m'tsogolo mwake, anthuwo sadabwerenso pa tsiku la sabata. Kenaka ndidaŵalamula Alevi kuti adziyeretse ndipo abwere kudzalonda pa zipata, kuti tsiku la sabata lisungike ngati lopatulika. Inu Mulungu wanga, mukumbukire zimenezinso pondikomera mtima, ndipo mundisunge potsata chikondi chanu chachikulu chosasinthika. Nthaŵi imeneyo ndidaona Ayuda amene adaakwatira akazi a ku Asidodi, a ku Amoni ndiponso a ku Mowabu. Mwakuti theka limodzi la ana ao ankalankhula chilankhulo cha ku Asidodi, sankathanso kulankhula Chiyuda, koma ankalankhula chilankhulo cha anthu a mitundu inayo. Tsono ndidakangana nawo ndi kuŵatemberera. Ndidamenya ena mwa iwo ndi kuŵazula tsitsi. Ndipo ndidaŵalumbiritsa m'dzina la Mulungu kuti, “Musadzakwatitse ana anu aakazi kwa amuna achilendo, ndipo ana anu aamuna ndi inu nomwe musakwatire akazi achilendo. Kodi Solomoni mfumu ya Aisraele suja adachimwa chifukwa cha akazi otereŵa? Pakati pa mitundu ya pansi pano panalibe mfumu yofanafana naye. Mulungu ankamkonda ndipo adamuika kuti akhale mfumu ya Aisraele onse. Komabe akazi achilendo adachimwitsa ngakhale iyeyo. Monga tsopano tizimva kuti inunso mumachita choipa chachikulu chomwechi cha kuipira Mulungu pomakwatira akazi achilendo?” Mmodzi mwa ana aamuna a Yehoyada, mwana wa Eliyasibu mkulu wa ansembe uja, anali atakwatira mwana wa Sanibalati wa ku Horoni. Nchifukwa chake ndidampirikitsa kuti achoke ku Yerusalemu. Inu Mulungu wanga, mukumbukire m'mene anthuwo adaipitsira unsembe wao ndi m'mene adanyozera chipangano chimene mudachita ndi Alevi. Umu ndimo m'mene ndidaŵayeretsera anthu poŵachotsera kalikonse kachilendo. Ndipo ndidakhazikitsa ntchito za ansembe ndi za Alevi, kuti aliyense adziŵe bwino ntchito yake. Chinanso, ndidalamula kuti nkhuni ndi zipatso zoyamba kucha azipereke pa nthaŵi yoyenera. Inu Mulungu wanga, mukumbukire zonsezi ndipo mundikomere mtima. Kudaali munthu wina, dzina lake Yobe, amene ankakhala m'dziko la Uzi. Munthu ameneyo anali wosalakwa ndiponso wolungama. Ankaopa Mulungu namapewa zoipa. Anali ndi ana aamuna asanu ndi aŵiri, ndi ana aakazi atatu. Anali ndi nkhosa 7,000, ngamira 3,000, ng'ombe zantchito 1,000 ndi abulu aakazi 500. Anali ndi antchito ambiri, choncho anali munthu wotchuka koposa anthu onse a m'maiko akuvuma. Ana ake aamuna ankachita phwando mosinthana, tsiku lina kwa wina, tsiku lina kwa wina. Ndipo ankaitana alongo ao atatu aja ku maphwando aowo. Tsono masiku a phwandowo akatha, Yobe ankadzuka m'mamaŵa napereka nsembe, kuperekera mwana aliyense, kuti anawo ayeretsedwe potsata malamulo a chipembedzo. Yobeyo ankati, “Mwina mwake, wina mwa ana angaŵa adachimwa, adatukwana Mulungu mumtima mwake.” Umu ndimo m'mene ankachitira Yobe nthaŵi zonse. Tsiku lina pamene angelo a Mulungu ankabwera kudzadziwonetsa pamaso pa Chauta, nayenso Satana adafika nawo limodzi. Pamenepo Chauta adafunsa Satanayo kuti, “Nanganso iwe Satana, kutereku ukuchokera kuti?” Iye adayankha kuti, “Ndakhala ndikungoyendayenda ndi kumangozungulira dzikoli.” Chauta adamufunsanso kuti, “Kodi wazindikirapo mtumiki wanga Yobe, kuti safanafana ndi wina aliyense pa dziko lapansi? Iye uja ndi munthu wosalakwa ndi wolungama. Amandimvera Ine Mulungu, ndipo amapewa zoipa.” Satana adafunsa Chauta kuti, “Kani mwayesa Yobe uja amangokumverani pachabe? Suja Inu mwakhala mukumteteza ponseponse iye uja, pamodzi ndi banja lake ndi zinthu zake zonse zimene ali nazo. Mudamdalitsanso pa ntchito zimene amachita, ndipo chuma chake nchochuluka kwambiri m'dzikomo. Koma tsopano tangoyesani kumchotsera zonse zimene ali nazo, muwona, adzakutukwanirani pamaso.” Chauta adauza Satana kuti, “Chabwino, zonse zimene Yobe ali nazo ndaziika m'manja mwako. Koma iye yekhayo usamkhudze.” Pamenepo Satanayo adachoka, kumsiya Chauta. Tsiku lina ana aamuna ndi ana aakazi a Yobe ankachita phwando m'nyumba mwa mkulu wao. Ndiye kudafika wamthenga kwa Yobe kudzamuuza kuti, “Ng'ombe zinalikulima, ndipo abulu analikudya pafupi pomwepo. Mwadzidzidzi nkubwera Aseba kudzatithira nkhondo nalanda ng'ombezo ndi abulu omwe. Ndipo apha antchito onse, koma ine ndekha ndiye ndapulumuka kuti ndidzakuuzeni.” Iyeyo akulankhulabe, padafikanso wina, nati, “Kunagwa mphezi ndipo yapsereza nkhosa zonse pamodzi ndi abusa omwe, onse psiti. Ine ndekha ndiye ndapulumuka kuti ndidzakuuzeni.” Ameneyu asanatsirize kulankhula, padafikanso wina, nati, “Kunafika magulu atatu a Akaldeya kudzatithira nkhondo. Atilanda ngamira zonse, ndipo apha antchito onse. Ndapulumukapo ndine ndekha kuti ndidzakuuzeni.” Iyeyo mau akali m'kamwa, padafikanso wina, nati, “Ana anu onse anali pa phwando m'nyumba ya mkulu wao. Mwadzidzidzi chayamba chimphepo champhamvu chochokera ku chipululu, nkudzaomba nyumbayo mbali zonse. Motero yagwa ndi kuŵapsinja anawo. Onse aphedwa, ndapulumukapo ndine ndekha kuti ndidzakuuzeni.” Yobe atamva zimenezo, adadzambatuka, nkung'amba zovala zake. Adameta tsitsi, ndipo adadzigwetsa pansi napembedza Mulungu. Adati, “M'mimba mwa amai ndidatulukamo maliseche, namonso m'manda ndidzaloŵamo maliseche, Chauta ndiye adapatsa, Chauta ndiyenso walanda. Litamandike dzina la Chauta.” Ngakhale zidaayenda motero, Yobe sadachimwe kapena kunena kuti, “Mulungu walakwa.” Tsiku lina pamene angelo a Mulungu ankabwera kudzadziwonetsa pamaso pa Chauta, nayenso Satana adafika nawo limodzi. Pamenepo Chauta adafunsa Satanayo kuti, “Nanganso iwe Satana, kutereku ukuchokera kuti?” Iye adayankha kuti, “Ndakhala ndikuyendayenda ndi kumangozungulira dzikoli.” Chauta adamufunsanso kuti, “Kodi wazindikirapo mtumiki wanga Yobe, kuti safanafana ndi wina aliyense pa dziko lapansi? Iye uja ndi munthu wosalakwa ndi wolungama. Amandimvera Ine Mulungu, ndipo amapewa zoipa. Iyeyo akali ndithu wokhulupirikabe kwambiri, ngakhale kuti iwe paja udaandiwumiriza kuti ndikulole kuti umuvutitse popanda chifukwa.” Apo Satana adayankha kuti, “Koma ayesedwe m'thupi mwake. Zinthu zonse zimene munthu ali nazo angathe kuzipereka, chikulu iyeyo ali moyo. Koma tsopano taonongani thupi lake, muwona, adzakutukwanirani pamaso.” Chauta adauza Satana uja kuti, “Chabwino, iyeyo uchite naye zonse zimene ukufuna, koma moyo wake wokha usauchotse.” Choncho Satana adachoka kumsiya Chauta napita kukazunza Yobe ndi zilonda zoopsa pa thupi lonse. Pamenepo Yobe adatenga phale kuti azidzikandira, nakakhala pa dzala. Tsono mkazi wake adamuuza kuti, “Ha! Mukukhalabe okhulupirika motere! Ingomtukwanani Mulunguyo, mufe basi!” Koma Yobe adauza mkazi wakeyo kuti, “Ukulankhula ngati mkazi wopusa. Ngati tilandira zokondweretsa kwa Mulungu, tilekerenji kulandiranso zoŵaŵa?” Motero pa zonsezi Yobe sadachimwe polankhula pake. Tsono abwenzi ake a Yobe, Elifazi wa ku Temani, Bilidadi wa ku Suki, ndi Zofari wa ku Naama, adazimva za masoka onseŵa amene adamgwera. Ndiye tsiku lina anthu atatuwo adabwera, aliyense kuchokera kwao. Onsewo anali atapangana za nthaŵi yoti adzampepese ndi kudzamsangulutsa. Ataona Yobeyo chakutali, sadamzindikire, ndipo adayamba kulira mofuula. Adang'amba zovala zao, nadzithira fumbi kumutu. Adakhala ndi Yobeyo masiku asanu ndi aŵiri, usana ndi usiku womwe. Koma panalibe ndi mmodzi yemwe amene ankalankhula naye, chifukwa chozindikira kuti Yobeyo akuvutika kwambiri. Pambuyo pake Yobe adalankhula, nayamba kutemberera tsiku lake lobadwa. Adati, “Tsiku limene ine ndidabadwa litembereredwe, nawonso usiku umene mai wanga adatenga pathupi pa ine utembereredwe. Tsiku limenelo lisanduke lamdima. Mulungu kumwambako asaliganizirenso tsiku limenelo, kuŵala kusadzaonekenso pa tsikulo. Tsikulo likhale la mdima wabii, likhale lamikhwithi, mdima wake ukhale woopsa. Usiku umenewo ukhale wa mdima wandiweyani. Tsiku limenelo lisakhalenso pamodzi ndi masiku a pa chaka, lisaŵerengedwerenso kumodzi ndi masiku a pa miyezi. Ndithu usiku umenewo usabweretsenso chabwino chilichonse, kusamvekeponso nthungulu zachikondwerero usikuwo. Odziŵa kutemberera masiku, alitemberere tsikulo, ndiye kuti odziŵa kuutsa Leviyatani, chilombo cham'nyanja chija. Nyenyezi zake zambandakucha zisaŵale. Tsikulo liyembekeze kucha, koma pachabe. Lisaonenso kuŵala kwa mbandakucha. Tsiku limenelo litembereredwe, chifukwa ndi limene ndidatuluka m'mimba mwa mai wanga, ndipo ndi limene lidandiwonetsa zovuta. “Bwanji sindidangobadwa wofaifa! Bwanji sindidangoti badwu nkufa! Chifukwa chiyani mai wanga adandifukata? Chifukwa chiyani adandiyamwitsa? Ndikadafa pobadwa pomwe, bwenzi ndikukhala nditagona mwaphee, kungogona tulo, ndi kumangopumula. Bwenzi ndikukhala limodzi ndi mafumu ndi aphungu a pa dziko lapansi, amene adadzimangira nyumba zikuluzikulu pa mabwinja akale. Bwenzi ndikukhala limodzi ndi mafumu okhuphuka, amene adadzaza nyumba zao ndi golide ndi siliva. Bwenzi sindidangokhala ngati mtayo woikidwa m'manda, ngati makanda amene sadaonepo kuŵala kwa dzuŵa. Kumandako anthu oipa savutitsanso, anthu otopa akupumula kumeneko. Am'ndende akupeza nawo mtendere kumeneko, sakumvanso mau ankhanza a kapitao wa ndende. Anthu wamba ndi apamwamba omwe ali pamodzi kumeneko, kapolo ndi womasuka kwa mbuyake. “Chifukwa chiyani dzuŵa limamuŵalira munthu wapamavuto? Chifukwa chiyani amakhalabe ndi moyo munthu wa mtima woŵaŵa? Amalakalaka imfa, koma osaiwona, amaifunafuna kupambana chuma chobisika. Amakondwa ndi kusangalala kwambiri akafa ndi kuikidwa m'manda. Chifukwa chiyani moyo umapatsidwa kwa munthu amene njira ya moyo wake yabisika, amene Mulungu wamzinga ndi mavuto ponseponse? M'malo moti ndidye, ndimalira, ndipo kubuula kwanga nkosalekeza. Zimene ndinkaziwopa zachitika ndithu, zimene ndinkachita nazo mantha zandigweradi. Ine sindipeza mtendere kapena bata, sindiwona mpumulo, koma mavuto okhaokha.” Tsono Elifazi wa ku Temani adati, “Iwe Yobe, kodi wina atakuyankha, ndiye kuti wakulakwira? Ah, koma ine ndekha sindingathe kukhala chete. Taona, iwe waphunzitsa anthu ambiri, walimbitsa mtima anthu ofooka. Mau ako adathandiza munthu wofuna kugwa, adachirikiza munthu wotha mphamvu. Koma tsopano mavuto akufikira iweyo, ndipo wataya mtima. Zakukhudza lero, ndipo ukuchita mantha. Unkalemekeza Mulungu, tsono uyenera kumdalira Iyeyo, Unkayenda m'njira yosalakwa, tsono uyenera kukhulupirira Mulungu. “Ganiza bwino tsopano: Kodi alipo munthu wosachimwa amene adaonongekapo nkale lonse? Nanga nkuti kumene udaona anthu olungama ataphedwa? Monga ndaonera ine, anthu amene amabzala tchimo namafesa mavuto, amakolola zomwezo. Monga momwe mphepo ya mkuntho imasakazira zinthu, Mulungu amaŵaononga ndi mkwiyo wake. Anthu oipa amakhuluma ngati mkango, koma Mulungu amaŵathyola mano. Iwowo amafa ngati mikango yosoŵa nyama, ndipo misona yao imamwazikana. “Tsono mau adandifika monong'ona, khutu langa lidamva kunong'onako. Zidandibwerera usiku m'masomphenya, nthaŵi imene anthu amagona tulo tofa nato. Ndidagwidwa ndi mantha, nkuyamba kunjenjemera, thupi langa lonse lidaweyeseka. Pamenepo mpweya wayaziyazi udandidutsa kumaso, ndipo ubweya wa pathupi panga udangoti njoo, kuimirira, chifukwa cha mantha. Chinthucho chidangoti chilili, koma ine osaŵazindikira maonekedwe ake. Patsogolo panga panali chinthu ndithu, kudangoti zii, kenaka ndidamva mau akuti: ‘Kodi munthu angathe kukhala wolungama pamaso pa Mulungu? Kodi munthu angathe kukhala wangwiro pamaso pa Mlengi wake? Mulungu sakhulupirira ndi atumiki ake omwe, angelo ake omwe amaŵapeza cholakwa. Nanji munthu amene adachokera ku dothi, amene ali fumbi chabe, amene amathudzuka ngati kadziwotche. M'maŵa ali moyo, madzulo nkufa munthuyo. Amapita ku manda, naiŵalika kotheratu. Zonse zimene ali nazo zimatha, ndipo amafa osadziŵa nkanthu komwe.’ ” “Iwe Yobe, itana tsono. Kodi alipo wina aliyense adzakuyankhe? Kodi ndi kwa mngelo uti ungapeze thandizo? Pajatu mkwiyo umapha chitsiru, ndipo njiru zimaononga wopusa. Ine ndidaona chitsiru chitamera mizu, koma mwadzidzidzi nyumba yake ndidaitemberera. Ana ake alibe nchitetezo chomwe, amaŵapondereza m'bwalo lamilandu, palibe wina aliyense woŵapulumutsa. Anthu anjala amamdyera zokolola zake, amamtengera ndi zapaminga zomwe. Anthu akhwinthi amafunkha chuma chake. Masautso satuluka m'fumbi, ndipo zovuta sizichokera m'dothi ai. Koma chibadwire munthu amangodzitengera mavuto yekha mosalephera, monga momwe sizilepherera mbaliwali kuulukira ku mlengalenga, kuchokera pa moto. “Achikhala ndinali ine, ndikadatembenukira kwa Mulungu, ndikadapereka mlandu wanga kwa Iye. Ntchito zake ndi zazikulu ndi zosamvetseka. Zodabwitsa zimene amachita ndi zosaŵerengeka. Amagwetsa mvula pa dziko lapansi, ndipo amathirira minda ya anthu. Amakweza anthu oluluka, ndipo amasangalatsa anthu olira. Amalepheretsa chiwembu cha anthu ochenjera, kotero kuti cholinga chao sichiphula kanthu. Amakola anthu ochenjera mu msampha wa kuchenjera kwao, amathetsa msanga zimene akapsala adakonza kuti achite. Iwowo amakumana ndi mdima ngakhale masana, amayambasa masanasana ngati usiku. Koma Mulungu amateteza amphaŵi kwa adani oŵasinjirira, amapulumutsa osauka kwa anthu ofuna kuŵapanikiza. Choncho amphaŵi amaŵalimbitsa mtima, koma anthu oipa amaŵatseka pakamwa. “Ndi wodala munthu amene Mulungu amamdzudzula. Nchifukwa chake usamanyoze chilango cha Mphambe. Pakuti ndiye amene amavulaza namangaponso mabala. Amakantha, komanso manja ake amachiritsa. Iye adzakupulumutsa ku masautso nthaŵi ndi nthaŵi. Zovuta sizidzakukhudza konse, zingachuluke bwanji. Pa nthaŵi ya njala adzakusamala, pa nthaŵi ya nkhondo adzakupulumutsa. Adzakuteteza kwa anthu osinjirira, chiwonongeko chikadzafika, sudzachiwopa. Pa nthaŵi ya chiwonongeko ndi ya njala uzidzaseka, zilombo zakuthengo sudzaziwopa. M'minda mwako simudzakhala miyala, nyama zakuthengo sizizakuvuta. Udzadziŵa kuti nyumba yako ndi malo amtendere, udzaona kuti pa zoŵeta zako palibe chosoŵa. Udzadziŵa kuti ana ako adzakhala ambiri, ndipo kuti zidzukulu zako zidzachuluka ngati udzu. Udzafika ku manda utakalamba, monga m'mene zokolola zimachera pa nyengo yake. Iwe Yobe, zonsezi ife tazifufuzafufuza, ndipo taona kuti ndi zoona. Uzimvere ndi kuzitsata zimenezi.” Tsono Yobe adayankha kuti, “Achikhala mavuto anga adaayesedwa, achikhala masoka anga adaaŵaika pa sikelo, bwenzi atalemera kupambana mchenga wonse wam'nyanja. Nchifukwa chake kulankhula kwanga kuli kokadzulira. Zoonadi mivi yake ya Mphambe yandibaya, thupi langa likumva ululu wa miviyo. Zoopsa za Mulungu zandizinga, kuti zilimbane nane. Kodi bulu amalira akakhala ndi msipu? Nanga ng'ombe, kodi imalira ikakhala ndi chakudya? Kodi chakudya nkuchidya chili zii, chopanda mchere? Kodi choyera cha dzira chimatsekemera? Zakudya zimenezi sindifuna nkuzilaŵa komwe, zakudya zake ndi zobwerera kukhosi. “Achikhala ndidaalandira chomwe ndikufuna, achikhala Mulungu adaandipatsa chimene ndikukhumba! Achikhala kudaamkomera Mulungu kuti anditswanye, achikhala adaandimenya ndi dzanja lake, nkundiwonongeratu! Zimenezi zikadandisangalatsa, ndikadakondwa nazo kwambiri ngakhale zipweteke chotani, podziŵa kuti sindidakane mau a Woyera uja. Kodi mphamvu zanga ndi zotani kuti ndizikhalabe ndi moyo? Nanga moyo wanga ukupitiriranji, ngati chiyembekezo palibe? Kodi ine ndidachita kuti gwa ngati mwala? Kodi thupi langa ndi lolimba ngati chitsulo? Zoona, ndilibenso mphamvu zodzipulumutsira, kulibenso kwina koti nkupezerako chithandizo. “Pa mavuto ngati ameneŵa pafunika abwenzi okhulupirika, kuwopa kuti mwina mwake munthu angasiyane ndi Mphambe. Koma abwenzi anga ndi onyenga, ngati mtsinje wothamanga, ngati mitsinje youma msanga mvula ikasoŵa. Ali ngati mitsinje ya madzi abii nthaŵi ya dzinja, imene madzi ake amakhala ambiri chifukwa cha kuchuluka kwa mvula. Koma pa nthaŵi ya mafundi imauma, kukatentha imamwerera. Anthu apaulendo amapatukirako kufuna madzi, koma amangoyendayenda nkufera m'chipululu. Oyenda pa ngamira a ku Tema amaifunafuna mitsinjeyo. Alendo a ku Sheba amaidalira. Amataya mtima chifukwa ankayembekeza kupeza madzi, koma pofika kumeneko, angoti kakasi, poti idauma. “Tsono umu ndimo m'mene inuyo mwandichitira ine. Mwaona tsoka langa, ndipo mukuchita mantha. Kodi ndanena kuti, ‘Mundipatse mphatso,’ kapena kuti, ‘Mupereke chiphuphu kwa wina chifukwa cha ine?’ Kodi ndanena kuti, ‘Mundipulumutse kwa mdani,’ kapena kuti, ‘Mundiwombole kwa ondizunza?’ “Chabwino, langizeni ndipo ndidzakhala chete. Dziŵitseni m'mene ndidachimwira. Mau oona amalasa mtima, koma inu mukunditsutsa pa zotani? Kodi inu mukufuna kundidzudzuliranji? Monga simukuwona kuti mau a munthu wotaya mtima ndi mphepo chabe? Zoonadi inu mumapondereza ana amasiye, ndi kuŵaika pa malonda abwenzi anu omwe. “Tsono mundiyang'anitsitse bwino! Sindikulankhula zabodza pamaso panu. Chonde, feŵani mtima, musachite zosalungama. Musandiimbe mlandu, poti ndine wolungama. Kodi mukuganiza kuti ndikulankhula zabodza? Monga ine sindingasiyanitse chabwino ndi choipa?” “Moyo wa munthu pa dziko lapansi ndi wa ntchito yakalavulagaga. Masiku ake ali ngati a munthu waganyu. Paja kapolo amalakalaka mthunzi, wantchito amayembekezera malipiro ake, ndiye inenso ndimangovutika nthaŵi zonse. Ngakhale usiku ndimapezabe mavuto. Ndikamagona ndimafunsa kuti, ‘Kodi kucha liti?’ Koma usiku ndi wautali, sindigona tulo, ndimangoti sadabusadabu mpaka mbandakucha. Thupi langa ladzaza mphutsi ndi zonyansa. Khungu langa lang'ambika, ndipo likudza mafinya. Masiku anga ndi othamanga kupambana makina oombera nsalu, amatha opanda chikhulupiriro chilichonse. “Inu Mulungu kumbukirani kuti moyo wanga uli ngati mpweya. Masiku abwino sindidzaŵaonanso. Amene akundiwona tsopano, sadzandiwonanso. Nthaŵi yomwe iye adzandifunafuna, ine ndidzakhala nditapita. Monga mtambo umazimirira ndi kukanganuka, momwemonso munthu woloŵa ku manda sabwerako. Sabweranso kunyumba kwake, ndipo onse omdziŵa amamuiŵala. “Nchifukwa chake sindidzatseka pakamwa. Ndiyenera kulankhula, chifukwa kukhosi kwanga kuli nthumanzi. Ndiyenera kudandaula, chifukwa mumtima mwanga muli zoŵaŵa. Kodi ine ndine nyanja, kapena chilombo cham'nyanja, kuti inu mundiikire alonda? Ndikagona pansi kuti ndithuze mtima, ndi kupeza mpumulo pabedi panga, inu mumandichititsa mantha ndi maloto, mumandiwopsa ndi zinthu zondiwonekera m'masomphenya. Choncho ndikadasankha kudzikhweza kapena kufa kumene, kupambana kupirira zovuta zimene ndikuzimva m'thupi mwanga. Ndatopa nawo moyo wanga, sindingakonde kukhala moyo nthaŵi zonse. Ingondisiyani, poti moyo wanga uli ngati mpweya chabe. Inu Mulungu, kodi munthu nchiyani, kuti muzimganizira chotere, kuti muzisamala zochita zake? Mumampenyetsetsa masiku onse, ndipo mumamuyesa nthaŵi zonse. Kodi mudzaleka liti kumandizonda, kuti ndingopezako mpata womeza malovu? Kodi ndikachimwa, ndimakuvutani bwanji, Inu Wopenyetsetsa anthu? Chifukwa chiyani mwandiika kuti ndikhale ngati choponyerapo chandamale chanu? Chifukwa chiyani ndikukhala ngati katundu wolemera kwa Inu? Chifukwa chiyani simukundikhululukira machimo anga ndi kundichotsera zolakwa zanga? Nthaŵi yoti ndiloŵe m'manda ili pafupi. Inu mudzandifunafuna, koma simudzandiwonanso.” Bilidadi. Apo Bilidadi, Msuhi, adayankha Yobe kuti, “Kodi udzakhala ukulankhulabe zoterezi mpaka liti? Mau akoŵa akungopita ngati mphepo. Kodi Mulungu amapotoza kuweruza kwake? Kodi Mphambe amalephera kuchita zachilungamo? Kapena ana ako adamchimwira, nkuwona Mulungu adaŵalanga chifukwa cha zochimwa zaozo. Ngati iwe uchita zimene Mulungu afuna, ngati upemba kwa Mphambe, ngati ukhala wangwiro ndi wolungama, ndithudi Mulungu adzachitapo kanthu, nkukuthandiza. Adzakubwezera zabwino zonse ngati mphotho yokuyenerera. Chiyambi chako chidzaoneka ngati chochepa, kuyerekeza ndi m'mene udzakhalira komaliza. “Tsono ndikukupempha kuti ufunsefunse kwa anthu amvulazakale, usinkhesinkhe zimene makolo athu adakumana nazo. Ife ndife adzulodzuloli, sitidziŵa kanthu ai. Moyo wathu pa dziko lapansi uli ngati chithunzithunzi. Kodi anthu amvulazakalewo nkupanda kukuphunzitsa? Kodi iwo nkupanda kukuuza zinthu? Pajatu mau a akulu akoma akagonera. “Kodi gumbwa nkumera pa nthaka yopanda chinyontho? Nanga bango nkukondwa kumene kulibe madzi? Popanda madzi zimenezi zimafota zikali zaziŵisi ndi zosadula, zimauma msanga kupambana chomera china chilichonse. Ndimo m'mene zimaŵachitikira anthu oiŵala Mulungu. Chikhulupiriro cha munthu wosapembedza Mulungu chimatha. Kulimba mtima kwake kumafooka, zimene amakhulupirira zili ngati ukonde wa kangaude. Amatsamira pa nyumba yake, koma nyumbayo si yolimba konse. Amaigwiritsa, komabe siikhalitsa. Munthu woipayo ali ngati zomera zokondwa ngakhale mpadzuŵa pomwe, ndipo nthambi zake zimatambalala pa munda wake. Mizu yake imayanga pa miyala, ndipo imakangamira pa thanthwe. Koma mutamchotsa pamalo pakepo, palibe ndi mmodzi yemwe angadziŵe kuti iyeyo anali pamenepo. Zokondwetsa zokhazo ndizo zidzakhala phindu la ntchito zake, kenaka ena adzabwera kudzaloŵa m'malo mwake. “Ndithu Mulungu sangamkane munthu wopanda cholakwa, komanso anthu olakwa Mulungu sangaŵathandize konse. Iye adzadzaza chiphwete m'kamwa mwako, ndipo udzafuula mokondwa. Amene amadana nawe adzachita manyazi, malo okhalako anthu oipa sadzaonekanso.” Yobe Tsono Yobe adayankha kuti, “Inde, ndikudziŵa kuti zimenezi ndi zoona, koma nanga munthu angathe bwanji kukhala wolungama pamaso pa Mulungu? Kodi wina aliyense angathe kutsutsana ndi Mulungu? Ai sangathe kutsutsana naye, chifukwa Mulungu ali ndi mafunso ambiri osayankhika. Mulungu ndi wanzeru, ndipo ndi wamphamvu kwambiri. Palibe munthu amene angathe kulimbana naye, popanda kupwetekerapo. Iyeyo amasendeza mapiri, iwo osadziŵako, amaŵagubuduza ali wokwiya. Ndiye amene amagwedeza dziko lapansi ndi zivomezi, ndipo mizati yake imanjenjemera. Ndiye amene angalamule dzuŵa kuti lisatuluke m'maŵa, ndi kuletsa nyenyezi kuti zisaŵale usiku. Ndi Mulungu yekha amene adayala zakuthambo, ndiye amayenda pa mafunde apanyanja. Ndiye amene adalenga nyenyezi za Mlalang'amba ndi Akamwiniatsatana, Nsangwe ndi Kumpotosimpita. Ndiye amene amachita zazikulu zosamvetseka, ndiye amene amachita zodabwitsa zosaŵerengeka. Ndithu Mulungu akapita pafupi ndi ine, sindimuwona konse. Akandidutsa, ine sindimpenya. Akamalanda zinthu, ndani angathe kumletsa? Ndani angathe kumufunsa kuti, ‘Mukuchita chiyani?’ “Mulungu sabweza ukali wake, adaononga adani ake othandizana ndi Rahabu, chilombo choipa chija. Nanga ineyo ndingathe kumuyankha bwanji? Mau okangana naye ndingaŵapeze kuti? Ngakhale ndine wosachimwa, sindingathe kumuyankha Mulungu. Ndiyenera kungopempha chifundo kwa Iye amene akundizenga mlandu. Ngakhale ndikadamuitana, Iye nkuvomera, sindikhulupirira kuti akadamvadi mau angawo. Paja amandikantha ndi mavuto onga mphepo yamkuntho, amandipweteka ndi mabala ambiri, popanda nchifukwa chomwe. Mulungu sandilola kuti ndipume, koma amandichulukitsirachulukitsira zoŵaŵa. Kodi ine nkulimbana ndi Mulungu, mphamvu zonse zija? Kodi ine nkutsutsana ndi Mulungu pa bwalo la milandu? Ndani angamuzenge mlandu? Ngakhale ndine wosalakwa, komabe zolankhula zanga zikhoza kunditsutsa. Ngakhale ndine wopanda cholakwa, akadandipezabe kuti ndine wolakwa. Ine ndiye ndilibe mlandu, koma sindidziyenereza, moyo wanga ndimaunyoza. Palibe chabwino ai. Nchifukwa chake ndikuti, Mulungu amaononga anthu oipa ndi anthu abwino omwe. Pamene munthu wosachimwa afa mwadzidzidzi, Mulungu amangoseka tsoka la munthu wosachimwayo. Mulungu akapereka dziko m'manja mwa anthu oipa, amaŵatseka maso anthu oweruza dzikolo. Ngati si Iyeyo wachita zimenezi, nanga nkukhala yani? “Masiku anga ndi othamanga kwambiri kupambana munthu waliŵiro. Masikuwo amapita, ine osaona zabwino. Amayenda ngati zombo zaliŵiro zapanyanja, ngati mphungu yogudukira nyama yoti idye. Mwina ndinganene kuti, ‘Ndidzaiŵala madandaulo anga, nkhope yanga sidzakhalanso yachisoni, ndipo ndidzasangalala.’ Koma ndimaopabe kuti mavuto anga onse adzabwereranso pa ine, pakuti ndikudziŵa kuti Mulungu sadzavomereza kuti ine ndine wosalakwa. Ngati ndine wolakwa ndithu, chabwinotu, zagwa zatha! Ngakhale ndisambe thupi lonse ndi madzi oyera kwambiri, ndi kusamba m'manja ndi sopo, Mulungu adzandiponyabe pa dzala, ndipo zovala zanga zomwe zidzachita nane nyansi. Zoona, Mulungu si munthu ngati ine, kuti ndingakangane naye, sindingathe kutsutsana naye pa mlandu. Palibe mkhalapakati woti nkutiweruza aŵirife, woti nkugamula mlandu pakati pa Mulungu ndi ine. Mulungu asandilange ndi ndodo yake, kuwopa Iye kusandidetse nkhaŵa. Motero ndidakatha kulankhula osamuwopa, koma monga zilirimu, sindingathe konse.” “Ndithudi, ndatopa nawo moyo wanga, choncho ndidzalankhula zodandaula zanga momasuka. Ndidzaulula zoŵaŵa zonse zamumtima. Ndidzauza Mulungu kuti, Inu Mulungu, musandiweruze kuti ndine wolakwa. Koma mundidziŵitse chifukwa chimene mukukanganirana nane. Kodi inu zikukukomerani kuti mundizunze ndi kundinyoza ine, ntchito ya manja anune, chonsecho mukukondera upo wa anthu oipa? Kodi maso anu ali ngati a munthu? Kodi mumaona zinthu monga m'mene amaziwonera munthu? Kodi masiku anu ndi aafupi monga m'mene aliri masiku a munthu? Kodi zaka zanu zili ngati zaka za munthu? Chifukwa chiyani tsono mukufufuza zolakwa zanga? Chifukwa chiyani mukufuna kundipeza mlandu? Koma chonsecho mukudziŵa bwino lomwe kuti ine ndine wosalakwa, kuti palibe ndi mmodzi yemwe amene angandipulumutse m'manja mwanu. “Mudandiwumba ndi kundipanga ndi manja anu. Koma tsopano mukufuna kundiwononga ndi manja anu omwewo. Musaiŵale kuti paja mudandipanga ndi dothi. Kodi mukufuna kundibwezeranso kufumbi komweko? Suja mudapatsa bambo wanga mphamvu zoti andibale, suja mudandikuza bwino m'mimba mwa mai wanga? Mudandikuta ndi khungu ndi mnofu, mudalumikiza mafupa anga ndi mitsempha. Mudandipatsa moyo mwa chikondi chanu chosasinthika, mudandisamala bwino kuti moyo wanga ulimbike. Nthaŵi yonseyo munkabisa zolinga zanu. Koma tsopano ndikuŵadziŵa maganizo anu. Munkapenyetsetsa kuti muwone ngati nditi ndichimwe. Munali wosafuna kukhululukira tchimo langa lililonse. Mukandipeza wolakwa, tsoka langa! Ngakhale mundipeze wosalakwa, ndigwetsabe nkhope, pakuti ndagwidwa ndi manyazi, poona mavuto angaŵa. Ndikadzilimbitsa mtima, mumakhala ngati mkango wondisaka, mumafuna kundiwopsa ndi mphamvu zanu. Mumandiikiranso mboni zondineneza, mkwiyo wanu umanka nukulirakulira. Magulu anu olimbana nane akunka nachulukirachulukira. “Inu Mulungu, chifukwa chiyani mudandibadwitsa ineyo? Achikhala ndidaangofa, wina aliyense asanandiwone. Achikhala ndidaachita ngati mtayo basi, akadanditenga pobadwapo nkupita nane ku manda. Kodi masiku a moyo wanga si oŵerengeka chabe? Ingondilekani kuti ndipumuleko pang'ono, ndisanapite kumene sindidzabwerako, dziko la imfa, kumene kuli mdima wandiweyani, ku dziko lamdimatu ndi lachisokonezo, kumene ngakhale kuŵala kudasanduka mdima.” Zofari Tsono Zofari wa ku Naama adayankha kuti, “Kodi mau ambirimbiriŵa nkukhala osaŵayankha? Kodi kulongolola nkumulungamitsa munthu? Iwe Yobe, kodi anthu nkukhala chete atamva kubwebweta kwakoku? Kodi ukamanyodola, sadzakhalapo wina aliyense wokudzudzula? Iwe umati mau akowo ndi oona, ukuti ndiwe wangwiro pamaso pa Mulungu. Koma ha, achikhala Mulungu adaalankhula, achikhala adaakudzudzula, achikhala adaakuululira zinsinsi za nzeru! Paja Iye uja nzeru zake ndi zozama zedi. Udziŵe tsono kuti Mulungu akukulanga pang'ono, mosalingana nkuchuluka kwa zolakwa zako. “Kodi iwe ungathe kumvetsa zinsinsi za Mulungu? Kodi ungathe kudziŵa kukula kwa nzeru za Mphambe? Malire a nzeru zake ali kutali kuposa mlengalenga. Nanga iwe ungachitepo chiyani? Malire a nzeru zake ndi ozama kupitirira dziko la anthu akufa. Nanga iwe ungathe kudziŵapo chiyani? Muyeso wa nzeru zake ndi wautali kupambana kutalika kwa dziko lapansi, ndi kupingasa kwa nyanja zamchere. Mulungu akabwera nakutsekera m'ndende, ndipo akakutulutsira ku bwalo la milandu, ndani angathe kumuletsa? Mulungu amazindikira anthu abodza. Pamene pali zolakwa, Iye uja nkupanda kudziŵa? Paja amati, Chitsiru nchitsiru ndithu, ndipo nyama ndi nyama ndithu. “Iwe Yobe, mumtima mwako ukhale wolungama, upemphe chifundo kwa Mulungu. Ngati mumtima mwako muli cholakwa, uchichotse, choipa chilichonse chisakhale m'moyo mwako. Ukatero, ndiye kuti manyazi ako onse adzatha, sudzazyolikanso pamaso pa anthu. Mtima wako udzakhazikika, ndipo sudzaopa kalikonse. Zoŵaŵa zakozi udzaziiŵala, zidzakhala ngati madzi amene apita kale. Pamenepo moyo wako udzaŵala kupambana dzuŵa. Usiku udzakhala ngati usana kwa iwe. Udzalimba mtima poti chikhulupiriro chilipo. Mulungu adzakutchinjiriza, ndipo udzapumula mwamtendere. Nthaŵi yogona palibe amene adzakuwopse. Ambiri adzakupempha kuti uŵachitire zabwino. Anthu oipa nawonso adzafunafuna thandizo, koma sadzaona njira yopulumukira, chiyembekezo chao ndi imfa basi.” Yobe Yobe adayankha kuti, “Inunso ndinu anthu, ndipo mukafa, nzeru zanu zidzafera nanu pamodzi. Koma inenso ndili nazo nzeru ngati inu nomwe. Inu simundipambana, ai. Aliyense amadziŵa zonse mwanenazi. Ine ndine chinthu choseketsa kwa abwenzi anga. Ine amene ndinkapemphera kwa Mulungu, Iye nkundiyankha, ine munthu wolungama ndi wopanda mlandu, tsopano ndine chinthu chochiseka. Munthu amene ali pabwino amanyoza mnzake amene ali pa tsoka. Tsokalo limagwa pa amene wayamba kale kugwa. Achifwamba ndiwo amakhala pa mtendere, amene amaputa Mulungu ndiwo amakhala pabwino. Anthuwo amadalira nyonga zao ngati ndiye Mulungu wao. “Koma ufunse kwa nyama zakuthengo, zidzakuphunzitsa. Ufunse mbalame zamumlengalenga, zidzakuuza. Upemphe nzeru kwa zolengedwa za dziko lapansi, zidzakuphunzitsa, ngakhale nsomba zam'nyanja zidzakufotokozera. Kodi mwa zonsezo nchiti chimene sichidziŵa kuti zonsezi adachita ndi Chauta? M'manja mwake ndimo muli zamoyo zonse, mulinso moyo wa anthu a mitundu yonse. Kodi suja khutu ndiye limamva mau, monga m'mene lilime ndiye limalaŵa chakudya? Inde anthu okalamba ali ndi nzeru, anthu amvulazakale ndi omvetsa zinthu. “Koma Mulungu ali ndi nzeru ndi mphamvu zopambana. Ali ndi uphungu wabwino, ndi kumvetsa zinthu zonse. Akapasula, palibe woti nkumanganso. Akatsekera munthu m'ndende, palibe woti nkumtsekulira. Akamanga mvula, dziko limauma, Akaimasula, madzi amasefukira pa dziko lonse. Iye ali ndi mphamvu, ndiponso ali ndi nzeru zonse. Anthu opusitsidwa, ndiponso opusitsa anzao, onsewo ali mu ulamuliro wake. Iye amalanda aphungu nzeru zao, ndipo amapusitsa aweruzi. Amamasula am'ndende a mafumu, ndipo amaŵamanga mafumuwo. Amasokeza ansembe ataŵalanda nzeru zao, ndipo amatsitsa atsogoleri amphamvu. Amakhalitsa chete aphungu okhulupirika, ndipo akuluakulu amaŵalanda luntha. Amanyoza anthu otchuka, ndipo anthu anyonga amaŵatha mphamvu. Amavundukula zamumdima, ndipo mdimawo amausandutsa kuŵala. Amakuza mitundu ina ya anthu, koma inanso amaiwononga. Amachulukitsa mafuko, nkuŵamwazanso. Amasandutsa atsogoleri kuti akhale zitsiru, ndi kumaŵayendetsa m'thengo mopanda njira. Iwowo amanka nafufuza njira mumdima mopanda kuŵala, nkumayenda ali dzandidzandi ngati oledzera.” “Zonse mukunenazi ndidaziwona ndi maso, ndidazimva ndi makutu anga, ndipo ndidazimvetsa. Zimene inu mumadziŵa, inenso ndimazidziŵa. Inu simundipambana ai. Koma ine ndikadakonda kulankhula ndi Mphambe, ndikadakonda kukamba naye Mulungu za mlandu wanga pamasompamaso. Inuyo ndinu okometsa zinthu ndi mabodza. Nonsenu muli ngati asing'anga apakamwa chabe. Achikhala munangokhala chete, apo mukadachita zanzeru Tsono mumve zimene nditi ndinene, mumvere mau anga ofotokoza za mlandu wanga. Kodi chifukwa chiyani mukunama potchula Mulungu? Chifukwa chiyani mukunena mabodza m'dzina lake? Kodi mukuti mukondere Mulungu? Kodi mukuti muteteze Mulungu pa mlandu wake? Mulungu atayang'anitsitsa inu, kodi nkukupezani kuti ndinu osalakwa? Kodi mungathe kumnyenga monga m'mene munthu anganyengere munthu mnzake? Ndithudi, adzakudzudzulani, mukamachita zokondera m'seri. Kodi ulamuliro wake sungakuwopseni? Kodi mphamvu zake sizingakuchititseni mantha? Miyambi yanuyi ndi yopandapake ngati phulusa. Zimene mukulankhula kuti mudzitchinjirize nazo zili ngati dothi. “Mukhale chete, ineyo ndilankhule, ndipo zimene zichitike, zichitike. Ndili wokonzeka kuika moyo wanga pa chiswe, kaya nkufa, ndife basi. Ngakhale Mulungu andiphe, ndidzamkhulupirirabe, ndipo ndidzafotokoza mlandu wanga pamaso pake. Kulimba mtima kwanga ndiye kudzandipulumutse, poti munthu woipa sangafike pamaso pa Mulungu. Mumvetsere mau anga mosamala, mutchere khutu zolankhula zanga. Mlandu wanga ndaukonza, ndikudziŵa kuti sadzandipeza wolakwa. Kodi pali yani amene angatsutsane nane? Ngati zili choncho, ndidakangokhala chete, nkufa basi. Inu Mulungu, ndikukupemphani zinthu ziŵiri zokha, sindidzayesa kukubisalirani. Muleke kundilanga, kuwopa Inu kusandidetse nkhaŵa. Mundiitane tsono ndipo ndidzayankha. Kapena mundilole kuti ndilankhule ndine, Inuyo mundiyankhe. “Kodi zolakwa zanga nzingati, ndipo machimo anga ndangati? Mundidziŵitse kulakwa kwanga ndi kuchimwa kwanga. Chifukwa chiyani mukundifulatira? Bwanji mukundiyesa mdani wanu? Kodi mukufuna kuwopsa ine, tsamba louluka ndi mphepone? Kapena mukuti mundithamangitse, ine mungu woumane? Inu mukundizenga zinthu zondiŵaŵa, umafukula ngakhale zolakwa za pa ubwana wanga. Inu mumamanga miyendo yanga ndi matangadza, mumalonda mayendedwe anga onse, mumazonda ndi poponda mapazi anga pomwe. Motero munthu amatha ngati chinthu chofumbwa, ngati chovala chodyewa ndi njenjete.” “Munthu wobadwa mwa mkazi amakhala masiku oŵerengeka, komanso masiku ake ndi amavuto okhaokha. Amaphuka ngati duŵa, kenaka nkufota. Sakhalitsa, amathaŵa ngati mthunzi. Kodi Inu Mulungu, mungamtuzulire maso woteroyo? Kodi mungamzenge mlandu? Ndani angatulutse chabwino m'choipa? Palibe ndi mmodzi yemwe. Masiku a munthu ndi oŵerengeka, chiŵerengero cha miyezi yake mumachidziŵa ndinu. Inu mudamulembera malire ake, sangathe kuŵalumpha. Mumleke tsono kuti apumule, akondweko, akondwerere moyo wake monga amachitira waganyu poweruka. “Mtengo chiyembekezo chake nchakuti akaudula udzaphukanso, nthambi zake sizidzaleka kuphuka. Ngakhale mizu yake ikalambe m'nthaka, ndipo chitsa chake chiwole, komabe chinyontho chikafika, udzaphukira, udzaphukadi nthambi ngati mtengo wanthete. Koma munthu akafa, kutha kwake nkomweko. Kodi munthuyo akafa, amapita kuti? Monga madzi amaphwa m'nyanja, monganso mtsinje umaphwa nuuma, momwemonso munthu amagona pansi osadzukanso. Mpaka zamumlengalenga zidzatha, iyeyo sadzadzuka. Palibe aliyense angamdzutse kutulo kwake. Ha! Achikhala mudaangondibisa ku manda, kuti ndisaoneke mpaka mkwiyo wanu utapita. Achikhala mudaangondiikira nthaŵi, kuti pambuyo pake mundikumbukirenso. Kodi munthu atafa, nkudzakhalanso ndi moyo? Koma masiku onse a moyo wanga wovutikawu, ndidzadikira mpaka kumasulidwa kwanga kutafika. Inu mudzandiitana, ine nkukuyankhani. Mudzafunitsitsanso kuwona ine, ntchito ya manja anune. Nthaŵiyo mudzayang'ana mayendedwe anga onse, koma simudzalondoloza machimo anga. Zolakwa zanga zidzakhululukidwa, Inu mudzafafaniza machimo anga onse. “Komabe monga phiri limagwa nkuswekasweka, ndipo thanthwe limasendezeka kuchoka pamalo pake, monganso madzi oyenda amaperesa miyala, ndipo madzi othamanga amakokolola nthaka, momwemonso Inu mumaononga chiyembekezo cha munthu. Mumamtswanya munthu kamodzinkamodzi, iye nkufafanizika kotheratu. Mumasintha maonekedwe a nkhope yake, nkumtaya kutali. Ana ake akamalemekezedwa, iye sadziŵako, akamachititsidwa manyazi, iye saziwona. Amangomva zoŵaŵa za m'thupi mwake zokha, amangodzilira yekha mwiniwakeyo.” Elifazi Apo Elifazi wa ku Temani adayankha kuti, “Kodi munthu wanzeru angalankhule zachabechabe motere? Kodi angathe kutulutsa mau opandapake ongouluka ngati mphepo? Kodi angathe kulankhula zinthu zopandapake, kapena kunena mau opanda phindu? Koma iwe ukufuna kuti anthu asamaope Mulungu, ukufuna kuti aleke kusinkhasinkha za Mulungu. Tchimo lako likuwonekera ndi kalankhulidwe kako, koma umafuna kudzilungamitsa ndi kuchenjera pakamwa kwako. Choncho ndi mau ako omwe amene akukutsutsa, osati ine. Pakamwa pako pomwe pakuchita umboni wokuzenga mlandu. “Kodi munthu woyamba kubadwa ndiwe? Kodi udaalipo pamene Mulungu ankalenga mapiri? Kodi uli m'gulu la alangizi a Mulungu? Kodi ukuyesa wanzeru ndiwe wekha? Kodi nchiyani chimene umadziŵa iwe, chosachidziŵa ife? Kodi chilipo chimene umamvetsa iwe, chosachimvetsa ife? Pakati pa ife pano tili ndi anthu aimvi ndi okalamba, amvulazakaletu kupambana bambo wako. Kodi akukuchepera mau othuzitsa mtima ochokera kwa Mulunguŵa, kapena mau okulankhula mofatsaŵa? “Nanga chifukwa chiyani ukupsa mtima? Chifukwa chiyani ukutituzulira maso? Chifukwa chiyani ukufuna kulimbana ndi Mulungu? Chifukwa chiyani ukumnyoza ndi pakamwa pako? Kodi munthu nchiyani kuti angathe kukhala wosachimwa? Kapena wobadwa kwa mkazi nchiyani, kuti angakhale wopanda uchimo pamaso pa Mulungu? Mulungu sakhulupirira ngakhale angelo ake. Ngakhale akumwamba omwe sali angwiro pamaso pake. Nanji tsono munthu, amene ali wonyansa ndi wachabechabe, amene kuchita zoipa kuli ngati kumwa madzi! “Undimve, ine ndikufotokozera, zimene ndidazimva ndikuuza. Zoonazo adandiphunzitsa ndi anthu anzeru, sadandibisire zimene adamva kwa makolo ao. Dziko lao linali lopanda anthu achilendo, amene adakaŵachotsa mu njira yake ya Mulungu. Munthu woipa amakhala akuvimvinika ndi zoŵaŵa masiku onse a moyo wake. Munthu wankhalwenso adzavutika zaka zake zonse. Amamva mau oopsa m'makutu mwake, pamene akuyesa kuti ali pabwino, achifwamba adzamthira nkhondo. Sakhulupirira kuti angathe kupulumuka ku mdima wa imfa, akuyenera kuphedwa ndithu basi. Amangoyendayenda paliponse, kunka nafuna chakudya nkumati, ‘Kodi chili kuti?’ Amadziŵa kuti tsiku lamdima lili pafupi. Masautso ndi nthumanzi zimamchititsa mantha kwambiri. Zimenezi zimamgudukira koopsa, monga imachitira mfumu imene yakonzekera kukamenya nkhondo. Zonsezi zamugwera chifukwa adaukira Mulungu. Adafuna kulimbana ndi Mphambe. Adatenga chishango chake mwaliwuma, ndipo adathamanga kuti akalimbane ndi Mulungu. “Ngakhale nkhope yake ndi yokulupala, ngakhale m'chiwuno mwake muli monenepa kwambiri, munthuyo adzasauka m'mizinda yoonongeka. Adzakhala m'nyumba zosayenera kukhalamo anthu, chifukwa zidaonongeka pa nkhondo. Iyeyo sadzalemera, chuma chake sichidzakhalitsa. Minda yake sidzaberekanso pa dziko lapansi. Iyeyo sadzatuluka m'mavuto, adzakhala ngati mtengo umene nthambi zake zapsa ndi moto, Umene maluŵa ake adzachotsedwa ndi mpweya wa Mulungu. Asadzinyenge pokhulupirira zinthu zoipa zachabe, poti zinthu zachabezo ndizo zidzakhale malipiro ake. Adzafota nthaŵi isanakwane, ndipo nthambi yake sidzaphukanso. Adzakhala ngati mtengo wamphesa umene umayoyola zipatso zake zisanapse. Adzakhala ngati mtengo wa olivi umene wayoyola maluŵa ake. Anthu osamvera Mulungu adzakhala opanda zidzukulu. Olandira ziphuphu moto udzapsereza nyumba yao. Ameneŵa ndiwo amalingalira zaupandu namachita zoipa. Mtima wao umaganizira zonyenga nthaŵi zonse.” Yobe adayankha kuti, “Zoterezi ndidazimva kale. Nonsenu ndinu anthu osatha kuthuzitsa mtima mnzanu. Kodi mudzakhala mukulankhulabe mau achabechabeŵa mpaka liti? Kaya chakuvutani nchiyani kuti muzilankhulabe mau otsutsaŵa? Inenso ndikadalankhula monga inu, mukadakhala monga ndiliri inemu. Inenso ndikadatha kulankhula monga mukulankhuliramu. Nanenso ndikadakupukusirani mutu. Ndikadakulimbitsani ndi mau anga, ndikadakuthuzitsani mtima ndi kuchepetsa zoŵaŵa zanu. “Ine ndikati ndilankhule, zoŵaŵa zanga sizichepa. Ndikati ndikhale chete, zoŵaŵazo zikhala zilipobe. Ndithudi, Mulungu wanditha mphamvu, waononga banja langa lonse. Wandigwira, ndipo wasanduka mdani wanga, umboni woti ndine wolakwa. Ndatsala mafupa okhaokha, ndipo chimenechi chikunditsimikiza kuti ndine wolakwa. Mulungu wanding'amba ali chikwiyire, ndipo akudana nane, wachita kulumira mano. Mdani wanga akundituzulira maso. Anthu amandinyoza polankhula, amandimenya pa tsaya mwachipongwe, akundichitira upo kuti alimbane nane. Mulungu wandipereka kwa anthu osasamala za Iye, wandiponya m'manja mwa anthu oipa. Ndidaali pa mtendere, koma Mulungu adanditswanya. Adandigwira pa khosi ndi kundiphwanya. Adandiimika kuti ndikhale choponyerapo chandamale chake. Mivi yake ikundilasa pa mbali zonse. Walasa impso zanga mopanda chifundo, watayira pansi ndulu yanga. Akundivulazavulaza. Akulimbana nane ngati munthu wankhondo. “Ndasokerera chiguduli pathupi panga. Ndaika mphamvu zanga pa fumbi. Maso anga afiira nkulira, ndipo zikope zanga zatupa kwambiri. Koma sindidachite chiwawa chilichonse, pemphero langa kwa Mulungu ndi lolungama. “Iwe, dziko lapansi, usabise zoipa zimene andichita. Kulira kwanga kofuna thandizo kusalekeke. Tsopano lino mboni yanga ili kumwamba, wonditchinjiriza ali komweko. Abwenzi anga akundinyodola, choncho ndikulirira kwa Mulungu. Kukadapezeka wondipepesera kwa Mulungu, bwenzi atandipepesera, monga momwe munthu amachitira mnzake. Pakuti zitapita zaka pang'ono, ndidzayenda njira imene sindidzabwerera. Mtima wanga wasweka ndipo masiku anga atha, manda andiyasamira kukamwa. Ndithudi, pali ondiseka ponseponse pondizungulira, ndikupenya m'mene akundinyozera. “Inu nokha Mulungu, mukhale ngati chigwiriro changa. Kulibenso wina woti nkunditchinjiriza. Inu mwatseka mitima yao kuti asamvetsetse bwino zanzeru, choncho musalole kuti iwowo apambane. Paja akuti munthu akapereka abwenzi ake chifukwa cha chuma, ana ake amazunzika. “Andisandutsa chisudzo chochiseka anthu, akandiwona amangoti malovu nzee. M'maso mwanga mwada ndi chisoni, ndaonda ndi mutu womwe. Anthu olungama akudabwa nazo kwambiri zimenezi. Anthu osachimwa akupsera mtima anthu osamvera Mulungu. Komabe anthu olungama enieni amapitirira m'njira zao, anthu osalakwa amalimbikira kukhalabe oyera. “Tsono nonsenu bwerani, mubwereze mau anu, pakati panupa sindidzapezapo ndi mmodzi yemwe wanzeru. Masiku anga atha, ndipo zimene ndidaakonza zalephereka. Zimene ndinkayembekeza zapita padera. Koma abwenzi anga amanena kuti usiku ndi usana womwe. Amati, ‘kuŵala ndiye kuli pafupi,’ chonsecho mdima uli goo. Chimene ndikuyembekeza ndicho kukakhala ku manda, ndikayaleko mphasa yanga mumdima. Ndidzauza dzenje la manda kuti, ‘Iwe ndiwe bambo wanga.’ Ndidzalankhulanso ndi mphutsi kuti, ‘Ndiwe mai wanga,’ kapena kuti, ‘Ndiwe mlongo wanga.’ Tsono chiyembekezo changa chili kuti? Ndani angaone populumukira panga? Ndithu, sindidzakhalanso ndi chiyembekezo chilichonse poloŵa m'manda, pamene ndidzatsikira ku fumbi.” Bilidadi Tsono Bilidadi wa ku Suki adayankha kuti, “Kodi iwe Yobe, ukhala mpaka liti ukufunafuna zonena? Ingokhala chete, umvetsere, ndipo ife tilankhula. Chifukwa chiyani ukutiyesa opusa ngati ng'ombe? Chifukwa chiyani tikuwoneka ngati opanda nzeru m'maso mwako? Iwe ukungodzipweteka ndi mkwiyo wako. Kodi dziko lapansi lidzasanduka bwinja chifukwa choti iweyo uli wokwiya? Kodi thanthwe nkudzachotsedwa pamalo pake, kuti likukondweretse iweyo? “Nyale ya munthu woipa yazima, malaŵi a moto wake sakuŵalanso. Kuŵala kwa m'nyumba mwake kwasanduka mdima, ndipo nyale ya pambali pake yazima. Kale ankayenda ndi mgugu, koma tsopano wakhumudwa. Nzeru zake zomwe zamgwetsa. Mapazi ake omwe amloŵetsa mu ukonde, ndipo wakodwa. Tsono kuti achokemo, wagweranso m'mbuna. Msampha wamkola mwendo, ndipo khwekhwe lamgwira. Amtchera msampha pansi mobisika, amtchera diŵa m'njira. Zoopsa zikumchititsa mantha pa mbali zonse, zikumtsatira pambuyo pake. Adaali ndi mphamvu, koma tsopano ali ndi njala. Tsoka likumdikira nthaŵi zonse. Wagwidwa nthenda yoopsa thupi lonse, miyendo yake, manja ake, zonse zaola. Amuchotsa m'nyumba mwake m'mene ankadalira. Amkokera kwa Imfa, mfumu ya zoopsa zonse. M'nyumba mwake zake zonse zachotsedwamo, awazamo sulufule, kuti aphe tizilombo ta matenda. Mizu yake ikuuma pansi, nthambi zake zikufota. Sadzamkumbukiranso kwao kapena kwina kulikonse, dzina lake lidzaiŵalika. Adzamchotsa m'dziko la amoyo ndi kumponya mu mdima, adzampirikitsa pa dziko lapansi. Sadzaona zidzukulu m'banja mwake. Sikudzaoneka ana otsala kumene ankakhalako. Anthu akuzambwe adabwa nalo tsoka lakelo, anthu akuvuma nawonso akungopukusa mitu. Ndithu zimenezi ndizo zimagwera anthu oipa. Kumeneku ndiye kutha kwake kwa anthu osasamala za Mulungu.” Yobe Tsono Yobe adayankha kuti, “Kodi mudzakhala mukundizunzabe mpaka liti? Chifukwa chiyani mukundilasa ndi mau anu? Mwakhala mukundinyoza kambirimbiri, Bwanji osachita manyazi kuti mukundisautsa? Ngakhale zitakhala zoona kuti ndachimwa, kuchimwakotu nkwanga. Ndithudi, mukuganiza kuti mukundipambana. Mukuti mavuto angaŵa akusonyeza kuchimwa kwanga. Koma tsono mudziwe kuti Mulungu ndiye wandichita zimenezi, ndiye amene wanditchera msampha umenewu. Ndithu, ndimafuula kuti, ‘Mayo, akundizunza ine!’ Koma palibe wondiyankha. Ndimapempha chithandizo, koma palibe wondichitira zolungama. “Mulungu wanditsekera njira, kotero kuti sindingathe kubzola. Njira yangayo waiphimba ndi mdima. Iye wandilanda ulemerero wanga, wandivula chisoti chaulemu. Wandiphwanyaphwanya mbali zonse, ndipo ndatheratu. Wandilanda chikhulupiriro changa, monga momwe amazulira mtengo. Mulungu wandikwiyira, akundiyesa ngati mdani wake. Watumiza ankhondo ake ochuluka kuti adzalimbane nane. Akonzekeratu zodzandithira nkhondo pafupi ndi nyumba yanga. “Mulungu waumiriza abale anga kuti andikane. Wasandutsa odziŵana nane kuti akhale achilendo kwa ine. Achibale anga andithaŵa. Abwenzi anga anditaya. Anthu odzacheza kunyumba kwanga andiiŵala, Antchito anga nawonso sakundilemekeza, ndasanduka ngati wakudza m'maso mwao. Ndikaitana wantchito, sandiyankha, ndimachita kupemba kuti andichitire kanthu. Ngakhale mkazi wanga yemwe amaipidwa nane. Ndine chinthu chonyansa kwa abale anga a mimba imodzi. Ngakhale ana omwe amandinyoza, ndikamayenda amandinyodola. Abwenzi anga onse apamtima amanyansidwa nane, amene ndinkaŵakonda kwambiri andiwukira. “Ndangoti gwa kuwonda, moyo wanga wapulumukira pang'onong'ono. Mvereni chifundo, chonde mvereni chifundo, inu abwenzi anganu, poti dzanja la Mulungu landikantha. Chifukwa chiyani mukundilondola ndinu ngati Mulungu? Kodi simudandizunze kokwanira? “Ha, achikhala ena adaakumbukira mau anga! Ha, achikhala mauwo adaalembedwa m'buku! Achikhala mauwo adaazokotedwa pa thanthwe ndi chitsulo, ndi kuthirapo mtovu kuti akhale mpaka muyaya! “Mtheradi ndikudziŵa kuti Momboli wanga alipo, ndipo pa nthaŵi yomaliza adzabwera kudzanditeteza. Khungu langa litatha nkuwonongeka, m'thupi langa lomweli ndidzamuwona Mulungu. Ine ndemwe ndidzamuwona, osati winanso ai. Ndidzamuwona ndi maso angaŵa. Mtima wanga ukulifunitsitsa tsikulo. Koma inu mukuti, ‘Ha, tingamzunze bwanji, popeza kuti zovuta zonsezi zaoneka chifukwa cha iye yemweyo?’ Inu muwope chilango, chifukwa ukali wa Mulungu umalangadi mosalephera. Motero mudzadziŵa kuti chiweruzo chilipo ndithu.” Zofari Zofari wa ku Naama adayankha kuti, “Iwe Yobe, wandipsetsa mtima. Nchifukwa chake ndikufulumira kuyankha. Ndikumva mau ondidzudzula ndi ondinyoza, koma ndadziŵa kale m'mene ndingathe kuyankhira. Kodi sukudziŵa zimene zidachitika masiku amakedzana, kuyambira nthaŵi imene munthu adalengedwa pa dziko. Kodi sukudziŵa kuti kukondwera kwa woipa nkosakhalira kutha? Kodi sukudziŵa kuti chimwemwe cha munthu wopanda Mulungu ncha kanthaŵi chabe? Ngakhale mbiri yake ifalikire ponseponse, ndipo ulemerero wake ukwere kufikira ku mlengalenga, adzatheratu monga momwe imatayikira ndoŵe yake. Amene ankamuwona azidzafunsa kuti, ‘Kodi uje uja ali kuti?’ Adzangozimirira ngati maloto, ndipo sadzapezekanso. Adzachotsedwa ngati zinthu zoonekera anthu kutulo usiku. Amene adamuwona kale sadzamuwonanso, sadzapezekanso kunyumba kwake. Ana ake adzabwezera zonse, zimene iyeyo adalanda anthu osauka. Thupi lake ndi la nyonga zaunyamata, komabe nyongazo zidzatha naye limodzi m'fumbi. “Zoipa zimakhala zozuna kwa iye, nchifukwa chake amachita ngati kuzisunga m'kamwa mwake. Ngakhale safuna kuleka kuzivumata, nangozisunga m'kamwa mwakemo, zoipazo akazimeza, zimaloŵa m'mimba mwake. Zimasanduka ngati ndulu ya mphiri m'kati mwa iyeyo. Amapeza chuma, koma amachisanzanso. Mulungu amachitulutsa m'mimba mwa munthuyo. Zimene amadya zili ngati ululu wa mphiri, ndipo ululuwo udzamupha. Sadzaona mitsinje ya mafuta a olivi, kapena mifuleni ya madalitso a m'dziko lamwanaalirenji. Adzabweza zimene adapata pogwira ntchito. Sadzadyerera chuma chake. Sadzapeza mpata wokondwerera phindu la malonda ake. Pakuti adapondereza amphaŵi ndi kuŵasiya osaŵasamala, ndipo adalanda nyumba zimene sadamange ndiye. “Chifukwa choti umbombo wake unali wosakata, sadzatha kusunga chilichonse chimene amakondwera nacho. Iyeyo ankati akadya, ankadyeratu zonse, tsono chuma chake chidatheratu. Ngakhale ndi wachuma, adzakhala mmphaŵi. Mavuto aakulu adzamgwera. Pa nthaŵi yoti adyerere chuma china, Mulungu adzamgwetsera ukali wamoto ngati mvula yosakata. Adzathaŵa mkondo wachitsulo, koma adzalasidwa chipyoza ndi muvi wamkuŵa. Muviwo atautulutsa m'thupi mwake, atachotsa nsonga yake yonyezemira yobaya ndulu yake, iyeyo adzagwidwa ndi mantha aakulu. Zonse zimene adazipeza, zazimirira ngati mu mdima. Moto wopanda woukwereza wamupsereza, watentha iyeyo pamodzi ndi zonse zotsalira m'nyumba mwake. Zamumlengalenga zidzaulula zolakwa zake, za pansi pano zidzamuukira. Chigumula cha madzi chidzaononga nyumba yake. Katundu wake yense adzachotsedwa pa tsiku la mkwiyo wa Mulungu. Izi nzimene Mulungu amasungira munthu woipa. Ndizo zimene Mulungu adalamula kuti zikhale mphotho ya munthuyo.” Yobe Tsono Yobe adayankha kuti, “Mumvetsere bwino zimene ndikulankhula, kunditonthoza mtima kwanu kukhale komweko basi. Loleni ndilankhuleko, ndikatha kulankhula, munditonzeretonzere. Kodi ine ndimadandaulira munthu? Tsono ndilekerenji kupsa mtima? Mundipenye, ndipo mudabwe, mugwire dzanja pakamwa. Ndikaganiza zimenezo, ndimachita mantha, ndimanjenjemera kwambiri. “Kodi anthu oipa amakhaliranji moyo? Bwanji amafika mpaka ukalamba, ndi kusanduka amphamvu pa ulamuliro? Amaona zidzukulu zao, ana ao amakula bwino iwo akupenya. Mabanja ao amakhala pabwino opanda mantha, mkwapulo wa Mulungu suŵakhudza nkomwe. Ng'ombe zao zamphongo zimabereketsa nthaŵi zonse, ng'ombe zao zazikazi sizipoloza. Ana ao amaseŵera pa bwalo, namavinavina ngati anaankhosa. Anawo amaimba, namaliza ng'oma ndi pangwe. Amakondwa pomva kulira kwa chitoliro. Masiku ao amatha iwowo akukondwa, amatsikira ku manda mwamtendere. “Anthuwo amauza Mulungu kuti, ‘Tichokereni! Sitifuna kudziŵa njira zanu. Kodi Mphambeyo ndaninso kuti tizimtumikira? Timapindula chiyani tikamapemphera kwa Iye?’ Iwowo akuti amapambana chifukwa cha ntchito zao. Koma ineyo maganizo amenewo sindigwirizana nawo. “Nkangati nyale ya oipa idazimapo? Nkangati tsoka limaŵagwera? Nkangati Mulungu amaŵakwiyira naŵalanga? Nkangati amaŵachotsa ngati phesi louluka ndi mphepo, ngati mungu wouluzika ndi kamvulumvulu? Paja amati, ‘Mulungu amalanga mwana chifukwa cha machimo a bambo wake.’ Ai, koma Mulungu aŵabwezere chilango ochimwawo, kuti adziŵedi kuti Mulungu ndiye amalanga ochimwa. Zoonadi ochimwawo alangidwe ndithu, alaŵe ukali wa Mphambe. Nanga kodi amalabadira chiyani za ana ao iyeyo atafa, chiŵerengero cha nthaŵi yake chitatha? Kodi alipo wina woti angaphunzitse Mulungu nzeru, poti Iyeyo amaweruza ngakhale anthu apamwamba? Ena amafa ali olemera kwambiri, ali pabwino, ndi pa mtendere. Ndi onenepa, thupi lao lili nenjenenje! Ndiponso ali ndi chuma chambiri. Koma ena amafa mtima wao uli woŵaŵa, osalaŵapo chabwino chilichonse. Koma olemera ndi osauka omwe onsewo amafa naikidwa m'manda, ndipo amagwa mphutsi. “Ndikudziŵa zimene mukuganiza, ndikudziŵanso chiwembu chanu chimene mukuti mundichite. Inu mumafunsana kuti, ‘Kodi nyumba ya mkulu uja ili kuti? Kodi hema limene munkakhala anthu oipa aja lili kuti?’ Kodi simudaŵafunsepo anthu oyenda mu mseu? Nanga kodi simuvomereza zimene iwowo amanena? Pa tsiku lakuti Mulungu alanga anthu, munthu woipa salangidwa konse. Amapulumuka pa tsiku loonekera mkwiyo wa Mulungu. Palibe ndi mmodzi yemwe amene amadzudzula munthu woipa, kapena kumbwezera zoipa zimene adachita. Pamene aikidwa m'manda, anthu amachezera pa manda ake. Anthu onse amatsatira mtembo wake. Amene amatsogola ndi osaŵerengeka, ndipo amakaika mtembo wakewo bwinobwino. Nanga inu mudzandisangalatsa bwanji ndi mau opanda pake? Zimene mwayankhazi ndi mabodza okhaokha.” Elifazi Tsono Elifazi wa ku Temani adayankha kuti, “Kodi munthu nkukhala waphindu kwa Mulungu? Iyai, munthu wanzeru amangodzipindulira yekha basi. Kodi Mphambe angapeze bwino chifukwa cha kulungama kwako? Kodi kapena Iyeyo nkupindulapo kanthu pa makhalidwe ako angwirowo? Kodi nchifukwa choti umamuwopa, kuti azikudzudzula, kuti azifuna kukukokera ku mlandu? Kodi osati nchifukwa choti kuipa kwako nkwakukulu, ndipo kulakwa kwako nkopanda malire? “Iwe unkaumiriza pachabe abale ako kuti apereke chikole, ndipo unkaŵalanda zovala zao, mpaka kuŵasiya ali ndi usiŵa. Anthu otopa sudaŵapatse madzi akumwa, anthu anjala udaŵamana chakudya. Chifukwa cha mphamvu zako udalanda dziko lalikulu, chifukwa cha kudzikonda udakhazikika m'menemo. Akazi amasiye udaŵachotsa opanda kanthu, ndipo ana amasiye udaŵapondereza. Nchifukwa chake misamphayi yakuzinga, ndipo wadzidzimuka ndi mantha. Kuli mdima ndipo sungathe kuwona kanthu, madzi achigumula akukumiza. “Kodi Mulungu sali kutalitali kumwamba? Ona nyenyezi zili m'mwamba kwambirizo, ona kutalika kwake pamene ziliripo! Komabe umanena kuti, ‘Kodi Mulungu amadziŵa chiyani? Wabisika ndi mitambo, nanga angatiweruze bwanji? Mitambo yakuda yamzinga, kotero kuti sangathe kuwona bwino, pamene akuyenda pamwamba pa thambopo.’ “Kodi iwe ukufuna kuyendabe m'njira yakale imene anthu oipa ankayendamo? Iwowo adachotsedwa nthaŵi yao isanakwane, maziko ao adakokoloka ndi madzi. Anthuwo ankauza Mulungu kuti, ‘Chokani pali ife pano!’ Adatinso, ‘Kodi Mphambeyo nkutichita chiyani ife?’ Chonsecho ndi Mulungu amene adaŵalemeretsa ndi zinthu zokoma. Nchifukwa chake ine ndekha ndiye maganizo a anthu oipa sindigwirizana nawo. Anthu abwino amaona zonse ndi kukondwa, anthu osachimwa amangoseka, akamaona oipa akulangidwa. Amanena kuti, ‘Ndithudi, adani athu aonongedwa, zimene adazisiya zaonongeka ndi moto.’ “Iwe Yobe, uziyanjana ndi Mulungu kuti ukhale pa mtendere, ukatero udzaona zabwino. Uzimvera malangizo amene Iyeyo amaphunzitsa, uziikapo mtima pa mau ake. Ubwerere kwa Mphambe modzichepetsa, uchotse zosalungama zonse zimene zimachitika m'nyumba mwako. Golide wako yense umuyese wachabechabe, ndithu, chuma chamtengowapatali uchiwone ngati dothi, Koma Mphambe ndiye akhale ngati golide wako, akhale ngati siliva wako wamtengowapatali. Ukatero udzakondwa naye Mphambe, Udzaikapo mtima pa Mulungu mwamtendere. Ukadzapemphera kwa Iye adzakumvera, udzapereka kwa Iye zija udalumbira kuti udzaperekazi. Chimene wachitsimikiza kuti udzachite, chidzachitikadi, kuŵala kudzakuunikira pa njira zako zonse. Pajatu Mulungu amagwetsa onyada, koma amapulumutsa odzichepetsa. Amapulumutsa munthu wopanda mlandu, adzakupulumutsa iwenso ndi kulungama kwako.” Yobe Apo Yobe adayankha kuti, “Leronso ndikudandaula kwambiri kwa Mulungu. Ngakhale ndikubuula, Mulungu akundilangiralangira ndithu. Ha, ndikadadziŵa kumene ndikadampeza Mulungu, kuti ndikafike mpaka komwe amakhalako! Ndikadakamba mlandu wanga pamaso pake, bwenzi nditafotokoza zifukwa zanga zonse. Bwenzi nditamva mau amene akadandiyankha, bwenzi nditamvetsa zimene akadandiwuza. Kodi Mulungu akadalimbana nane ndi mphamvu zake? Ai, koma akadamva mau anga. Kumeneko munthu wolungama akadalankhula ndi Iye modekha. Wondiweruzayo akadandipeza wosalakwa nthaŵi zonse. “Taonani, ndikapita chakutsogolo, Iye kulibe kumeneko, ndikabwerera cham'mbuyo, sinditha kumupenya. Ndimamfunafuna kumanzere, koma osamuwona. Ndimayang'ananso kumanja, koma osampenya ndithu. Komabe Mulungu amadziŵa m'mene ndimayendera, akandiyesa adzapeza kuti ndine wangwiro ngati golide. Mapazi anga akuponda m'mapazi mwake, ndasunga njira yake, ndipo sindidaitaye. Sindidapatuke kusiya malamulo ake. Ndasunga mau a pakamwa pake kupambana zofuna zanga zonse. “Iyeyo ndi wosasinthika, nanga ndani angathe kumsintha maganizo? Zimene wafuna, amazichitadi. Zimene adatsimikiza kuti adzandichita, adzachitadi, ndipo amalingalira zambiri zoterezi. Nchifukwa chake ndikuchita mantha kwambiri pamaso pake. Ndikaganiza za iyeyo, ndimaopa kwabasi. Mulungu walefula mtima wanga. Mphambe wandiwopsa. Wandichititsa mantha ndi Mulungu, osati mdima wa mavuto onse amene amandiphimbaŵa.” “Chifukwa chiyani Mphambe saikiratu nthaŵi yoti aweruze? Chifukwa chiyani amene ali olungama saŵaona masiku otero? Anthu ena amasendeza malire, kuti akuze dziko lao, amalanda ziŵeto namakazidyetsa ku mabusa ao. Amalanda abulu a ana amasiye, amalandanso ng'ombe za akazi amasiye, kuti zikhale chikole. Amapatutsa anthu osauka m'miseu, ndipo amapirikitsa amphaŵi onse. Amphaŵiwo amakafunafuna chakudya ku chipululu ngati mbidzi. Kulibe kwina koti apezere ana ao chakudya. Amakolola za m'minda ya eniake, amakunkha mphesa m'minda ya anthu oipa. Amagona maliseche usiku wonse, pa nthaŵi yozizira amasoŵa chofunda. Amavumbwa ndi mvula yakumapiri, amakangamira ku thanthwe chifukwa chosoŵa pousa. Palinso ena amene amatsomphola ana a masiye ku bele, ndipo amagwira ana a mmphaŵi kuti akhale chikole. Amphaŵi amangoyenda maliseche kusoŵa chovala, amasenza mitolo ya tirigu ali ndi njala. Amayenga mafuta a olivi m'minda ya anthu oipa, namapsinya mphesa, koma nkumamvabe ludzu. Anthu amene alikufa akubuula mumzindamo, anthu ovulala akulirira chithandizo. Komabe Mulungu sakusamalako mapemphero ao. “Pali ena amene amakana kuŵala, safuna kuyenda m'kuŵalako, ndipo sadziŵa njira zake. Wopha anzake amadzuka usiku kuti aphe osauka ndi amphaŵi. Nthaŵi ya usiku ena amasanduka mbala. Munthu wachigololo amadikira chisisira, namanena kuti, ‘Palibe woti angandiwone,’ ndipo amadzizimbaitsa nkhope. Mbala zimathyola nyumba usiku, masana zimadzitsekera, ndiye kuti zimapewa kuŵala. Onsewo kukada kwambiri, ndiye kuti kwaŵachera. Zoopsa za mdima woti goo ndiye bwenzi lao. “Munthu woipa amatengedwa ndi madzi a chigumula. Minda yake njotembereredwa m'dziko lonse. Sapitako kukagwira ntchito ku minda yake yamphesa. Monga momwe amasungunukira matalala nkuloŵa pansi chifukwa cha fundira, ndimo m'mene munthu wochimwa adzatsikire ku dziko la akufa. Ngakhale mai wake adzamuiŵala, koma mphutsi zidzasangalala pomudya. Momwemonso woipayo adzathyoka ngati mtengo. “Zidzatero chifukwa choti adaŵachita nkhanza akazi amasiye, akazi opanda ana sadaŵachite zabwino. Koma Mulungu amaononga anthu amphamvu. Anthuwo ngakhale atakhazikika, moyo wao ndi wosatsimikizika. Mulungu angathe kumtchinjiriza munthu woipa ndi kumpatsa mtendere, koma amakhala akupenyetsetsa njira zake. Woipayo amamkweza pa kanthaŵi kochepa, koma posachedwa saonekanso. Monga ena onse nayenso amafota ngati udzu, amagwa ngati ngala za tirigu akazidula. Ndani angathe kukana kuti si momwemo? Kodi wina anganditsutse kuti mau angaŵa si oona?” Bilidadi Apo Bilidadi wa ku Suki adayankha kuti, “Mulungu ali ndi ulamuliro wonse, ndipo anthu onse ayenera kumuwopa. Akusungitsa mtendere mu ufumu wake Kumwambamwambako. Kodi magulu ake ankhondo akumwamba ndi oŵerengeka? Kodi kuŵala kwake sikuŵala paliponse? Kodi alipo munthu wosachimwa pamaso pa Mulungu? Kodi munthu wobadwa mwa mkazi angakhale bwanji wosapalamula? Ngati mwezi sutha kupereka kuŵala kwenikweni, ndipo ngati nyenyezi sizitha kunyezemira pamaso pake, nanji tsono munthu amene ali ngati mphutsi chabe, nanji mwana wa munthu amene ali ngati nyongolotsi yam'dothi?” Yobe Tsono Yobe adayankha kuti, “Iwe, kodi wandithandiza ine munthu wosauka ndi wofookane ngati? Kodi wandilangiza zabwino ine, munthu wopanda nzerune ngati? Kodi wandiwuza nzeru zambiri pamenepa ngati? Kodi ndani adzamva mau akoŵa? Nanga udazitenga kuti zonsezi? “Mizimu ya anthu akufa ikunjenjemera pansi pa nthaka, zonse zokhala m'madzi pansipo zikuvutika. Dziko la anthu akufa ndi lapululu pamaso pa Mulungu, ndipo kumeneko sikuphimbika kwa Iye. Mulungu adayala thambo lakumpoto pa phompho, adakoloŵeka dziko lapansi m'malo mwake, pamene panali popanda nkanthu komwe. Amasunga madzi ambiri m'mitambo yochindikira, koma mitamboyo sing'ambika. Amaphimba mwezi, amauphimba ndi mtambo wake. Madzi Mulungu adaŵalembera malire onga uta, motero adalekanitsa kuŵala ndi mdima. Mizati yochirikiza thambo lakumwamba imanjenjemera ndi mantha, imazizwa pakumva kudzudzula kwa Mulungu. Ndi mphamvu zake adatontholetsa nyanja, ndi nzeru zake adakantha chilombo cham'madzi chija cha Rahabu. Ndi mpweya mwake adayeretsa zamumlengalenga, ndi dzanja lake adapha chinjoka chothaŵa chija. Zimenezi ndi pang'ono chabe za makhalidwe ake. Tingomva pang'ono za Iye ngati kunong'ona. Koma ndani angadziŵe kukula kwa mphamvu zake?” Yobe adapitiriza kulankhula nati, “Pali Mulungu wamoyo amene wakana kundiweruza molungama, pali Mphambe amene wandipweteketsa mtima. Nthaŵi zonse pamene ndikupumabe, Mulungu namandipatsa mpweya wa moyo, pakamwa panga sipadzatuluka mau oipa, lilime langa silidzalankhula zonyenga. Zakuti mukunena zoona, ine sindikuvomera. Kunena za ine ndidzakhalabe wokhulupirika mpaka kufa kwanga. Sindidzaleka kunena kuti ndine wolungama, sindidzasintha maganizo anga. Mtima wanga sukunditsutsa pa chinthu chilichonse. “Adani anga ziŵaonekere zinthu zoyenerera anthu oipa. Ondiwukira alangidwe monga momwe amachitira osalungama. Nanga chiyembekezo cha munthu wopanda Mulungu nchiyani pamene aphedwa, pamene Mulungu amchotsera moyo wake? Kodi Mulungu angamve kulira kwa munthu wotere, pamene zovuta zimgwera? Kodi angakondwere ndi Mphambe? Kodi angapemphere kwa Mulungu nthaŵi zonse? “Ndidzakuphunzitsani za mphamvu zazikulu za Mulungu, ndidzakusimbirani zimene Mphambe adakonza. Ndithu, inu mwadziwonera nokha, nanga bwanji mukulankhula zachabe? “Chilango chimene Mulungu amasungira munthu woipa, choloŵa chimene munthu wozunza anzake amalandira kwa Mphambe ndi ichi: ana ake ngakhale achuluke chotani, adzaphedwa ndi lupanga, zidzukulu zake zidzasoŵa chakudya. Amene adzamtsalireko adzafa ndi matenda, akazi ao amasiye sadzaŵalira. Ngakhale aunjike siliva ngati fumbi, kapena kukundika zovala ngati mchenga, koma olungama ndiwo amene adzavala zimenezo, ndipo anthu osachimwa adzagaŵana siliva ameneyo. Nyumba imene akuimanga ili ngati ukonde wa kangaude, ili ngati msasa umene mlonda amamanga. Amapita ku bedi ali wolemera, koma kutha kwake nkumeneko, poti aphenyule maso, angoona chuma chakecho pali ng'wa! Zoopsa zimamkokolola ngati madzi a chigumula, ndipo usiku mkuntho umamnyamula. Mphepo yakuvuma imamuulutsa, iye nkuzimirira, imamchotsa pamalo pake. Imakuntha pa iye osamchitira chifundo, pamene iye akuyesa kuithaŵa mwaliŵiro. Koma mphepoyo imamuwomba ndithu, ndipo kuchokera pamalo pake imamuwopseza.” Nyimbo yotamanda Nzeru. “Ndithudi, ulipo mgodi wa siliva, alipo malo oyengerapo golide. Chitsulo amachikumba pansi, mkuŵa amachita kuusungunula ku miyala yamkuŵa. Anthu amaloŵa mu mdima atatenga nyale namafunafuna miyalayo mpaka ku malire a mgodiwo, akuyenda mu mdima wandiweyani. Amakumba njira zapansi mumgodimo, kutali ndi kumene kumakhala anthu, mpaka kuiŵalika ndi anthu onka nayenda, amakhala ali lende pansipo, namazunguzika uku ndi uku. Nthaka imatulutsa chakudya, koma kunsi kwake kumachita ngati kofwantchuka ndi moto. Miyala yamumgodimo ndi ya safiro, mulinso fumbi la golide. “Njira ya mu mgodi imeneyi, palibe mbalame yodya zinzake imene imaidziŵa, kamtema yemwe sanaiwone. Zilombo zolusa sizinapondemo m'njiramo. Mkango sunadzeremo m'menemo. “Anthu amaphwanya matanthwe olimba, amagadabula mapiri kuyambira m'tsinde. Amasema mipita m'matanthwemo, ndipo amatulutsamo miyala ya mtengo wapatali. Amaletsa mitsinje yapansipo kuti isayende, motero amaonetsa poyera zinthu zobisika. “Koma nzeru zingapezeke kuti? Luntha lingapezeke kuti? Anthu sadziŵa kufunika kwake kwa nzeruzo, ndipo sizipezeka pa dziko lino lapansi. Phompho likuti, ‘Sizipezeka mwa ine muno,’ nyanja ikuti, ‘Mwa ine munonso ai.’ Nzeru sangazipate ndi golide, mtengo wake sangauyerekeze ndi siliva wambiri. Ngakhale golide wokoma kwambiri wa ku Ofiri sangafike pa mtengo wa nzeruzo, miyala ya onikisi kapena ya safiro nayonso singafikepo. Golide ndi mwala wagalasi sizingakwanire kuti agulire nzeru. Nzeru sangazisinthanitse ndi zokometsera za golide weniweni. Mtengo wake wa nzeru ndi woposa miyala ya korali ndi krisitala, umapambananso ndi miyala ya rubi yomwe. Mtengo wake wa nzeru umapambana ndi ngale zomwe. Miyala ya topazi ya ku Etiopiya sungaiyerekeze ndi nzeru, ngakhale golide wabwino kwambiri sangafikepo pa nzeru. “Kodi tsono nzeru zimachokera kuti? Nkuti kumene tingapeze luntha? Malo ake ndi obisika kwa zamoyo zonse, ndi obisikanso kwa mbalame zamumlengalenga. Ngakhale malo a chiwonongeko ndiponso imfa zimangoti, ‘Tidangomva mphekesera chabe ya zimenezo.’ “Mulungu yekha ndiye amadziŵa njira yake yopita kumeneko, amadziŵa kumene nzeruzo zimakhala. Paja Iye amayang'ana mpaka ku mathero a dziko lapansi, amaona zonse zimene zili kunsi kwa thambo. Pamene Iye adapatsa mphepo mphamvu zake, nayesa kuzama kwa nyanja, pamene adakhazika lamulo loti mvula izigwa, nakonza njira za ching'aning'ani cha bingu, pamenepo mpamene adaona nzeruzo naziyesa mtengo wake, ndipo adazikhazikitsa ndi kuzisanthula bwino lomwe. Choncho adauza munthu kuti, ‘Kuwopa Ambuye ndiye nzeru zimenezo, kuthaŵa zoipa ndiye luntha limenelo.’ ” Yobe Yobe adapitiriza nati, “Ha, ndikadabwerera mwakale monga m'mene ndinkakhalira pa nthaŵi yamakedzana, pa masiku amene Mulungu ankandisunga bwino. Nthaŵi imeneyo Mulungu anali nane, nyale yake inkandiwunikira mu mdima. Masiku amenewo ndinali pabwino zedi, madalitso a Mulungu anali pabanja panga. Nthaŵi imeneyo Mphambe anali nane, ana anga ali kwete m'mbalimu. Nthaŵi imeneyo ng'ombe ndi mbuzi zanga zinkandipatsa mkaka wambiri, mitengo yanga ya olivi inkamera ndi m'matanthwe momwe. Pamene ndinkapita ku chipata cha mzinda, pamene ndinkakonzekera zokakhala nawo pabwalopo, anyamata akandiwona ankapatuka, ndipo madoda ankadzambatuka nkukhala chilili. Akalonga ankakhala chete, atangoti pakamwa gwirire. Atsogoleri ankangoti duu, lilime litangoti nganganga ku nkhama. Aliyense womva za ine, ankanditchula kuti ndine wodala, aliyense wondiwona ankandilemekeza. Zidatero chifukwa choti ndinkapulumutsa amphaŵi olira, ndinkalanditsa ana amasiye opanda woŵathandiza. Anthu amene anali pa zoopsa kwambiri ankanditamanda, akazi amasiye ndinkaŵasangalatsa. Nthaŵi zonse ndinkachita zoyenera, ntchito zanga zonse zinali zangwiro. Ndinali ngati maso kwa anthu osapenya, ndinali ngati mapazi kwa anthu opunduka. Osauka ndinali ngati bambo wao, anthu osaŵadziŵa konse ndinali mtetezi wao pa milandu. Ndinkaononga mphamvu za anthu ankhalwe, ndinkalanditsa amene anali atagwidwa. “Tsono mumtimamu ndinkati, ‘Ndidzafera pakati pa ana anga, masiku a moyo wanga ndidzaŵachulukitsa kwambiri ngati mchenga. Ndinali ngati mtengo umene mizu yake yatambalalira ku madzi umene masamba ake ndi onyowa ndi mame. Aliyense ankandilemekeza, nthaŵi zonse mphamvu zanga zinali ngati uta wolimba.’ “Anthu ankamvetsera zimene ndinkanena, ankadikira atakhala chete kuti amve malangizo anga. Ine nditalankhula, iwowo sankalankhulanso, mau anga ankaŵagwira mtima. Ankayembekeza ine monga momwe amayembekezera mvula, ankangoti kukamwa yasa ngati anthu odikira mvula yam'malimwe. Ndinkaŵasekerera pamene iwowo analibenso chikhulupiriro, kukoma mtima kwanga kunkaŵalimbitsa mtima. Ndinkasankhula njira yao, ndipo ndinkaŵatsogolera ngati mfumu, tsono ndidakhazikika pakati pao, ngati mfumu pakati pa ankhondo ake, ndinali ngati msangalatsi pakati pa olira.” “Koma tsopano akundiyesa chinthu chochiseka, anthu amene ali ana kwa ine, anthu oti ndi atate ao omwe sindikadaŵayesa oyenera kuti athandizane ndi agalu kuŵeta nkhosa zanga. Kodi mphamvu zao zikadandipinduliranji, anthu amene nyonga zao zidatha kale? Anali atatheratu kuwonda ndi njala, natsala mafupa okhaokha, ankakungudza nthaka youma yachipululu. Ankathyola therere ndi masamba a zitsamba, ankadya mizu ya dinde. Ankaŵapirikitsa pakati pa anthu, anzao ankaŵakuwa ngati mbala. Ankaumirizidwa kumakhala m'zigwembe za mitsinje, m'maenje am'nthaka ndi am'matanthwe. Ankalira ngati nyama kuthengo, ndipo ankaunjikana pamodzi pa zitsamba zaminga. Iwowo anali opusa, achabechabe okhaokha, ndipo adaŵachotsa m'dziko. “Tsopano ine ndasanduka nyimbo yao, ndasanduka chisudzo chao. Ineyo ndimaŵanyansa, ndipo amandithaŵa. Akangondiwona, salephera kuti malovu nzee m'maso mwangamu. Poti Mulungu adandifooketsa ndi kundichepetsa, iwowo adalekeratu kundiwopa. Ku dzanja langa lamanja anthu achiwawa akundiwukira, akukumba mbuna yoti ndigweremo, akukonzekera njira zondiwonongeratu. Akunditsekera njira, ndipo akufuna kundichititsa ngozi, palibe wina aliyense woŵaletsa. Akundithamangira ngati madzi oloŵera pa linga logumuka, akubwererabwerera pakati pa chipasupasu. Zoopsa zandigwera. Ulemu wanga wachita ngati kuuluzika ndi mphepo, chuma changa chija chazimirira ngati mtambo. “Tsopano mtima wanga wachokamo. Ndili pa mavuto, ndilibe popumira. Mafupa anga akuphwanya usiku, zoŵaŵa sizikuleka. Chovala changa chakwinyikakwinyika chifukwa cha matenda, chikundithina ngati khosi la mkanjo wanga. Mulungu wandiponya m'matope, ndasanduka ngati fumbi ndi phulusa. “Ndimalira kwa Inu Mulungu, koma simundiyankha. Ndimapemphera, koma inu simundiyang'anako. Inu mwandichita zankhanza, mwandizunza ndi dzanja lanu lamphamvu. Inu mwandiika pa mphepo, mwandinyamula ndi mphepoyo, ndipo mwandiponya mu mkuntho wa namondwe. Tsono ndikudziŵa kuti Inu mudzandifikitsa ku imfa yanga, kumene aliyense adzapitako. “Komabe kodi munthu wam'mazunzo satambalitsa dzanja? Kodi salira chithandizo m'mavuto mwakemo? Kodi ine sindidalire nawo anzanga amene anali pa mavuto? Kodi mtima wanga sudaŵamvere chisoni anthu osauka? Koma pamene ndinkayembekeza zabwino, zovuta ndiye zimene zidandigwera. Pamene ndinkayembekeza kuŵala, mdima ndi umene udandiphimba. Mtima wanga ukuŵaŵa, ndikusoŵa mpumulo, masiku onse ndili pa mavuto. Ndikuyenda mu mdima popanda dzuŵa konse. Komabe ndimaimirira pa msonkhano ndi kupempha chithandizo molira. Kulira kwanga kuli ngati kwa nkhandwe, ndimakhala ndekha ngati nthiŵatiŵa. Khungu langa likuyamba kuda ndi kunyenyeka, Mafupa anga akutentha ndi chitungu. Pangwe wanga wasanduka woimbira maliro, chitoliro changa chikupolokeza anthu olira.” Yobe avomera kuchimwa kwake. “Ndidalonjezana ndi maso anga, ndikadatha bwanji kupenyetsetsa namwali? Kodi Mulungu kumwamba akadandisungira zotani? Kodi Mphambe kumwamba akadandikonzera zabwino zanji? Wosalungama tsoka limamgwera, wochita zoipa amaonongeka. Koma Mulungu amaona zochita zanga, amadziŵa mayendedwe anga onse. “Sindidachite zachiphamaso, sindidayesepo kunyenga anthu. Mulungu andiyese pa sikelo ya chilungamo, adziŵe kuti ndine wangwiro. Ngati mayendedwe anga asempha njira, ngati mtima wanga wakhumbira zinthu molakwa, ndipo ngati ndachita choipa chilichonse, pamenepo zimene ine ndidabzala adye ndi ena, zomera zanga zizulidwe. “Ngati mtima wanga udanyengedwapo ndi mkazi, ndipo ngati ndidalalira pa khomo la mnansi wanga, pamenepo mkazi wanga aphikire mwamuna wina chakudya, ndipo azigona naye. Pakuti limenelo likadakhala tchimo loopsa zedi, ukadakhala mlandu umene oweruza amaperekapo chilango chachikulu. Kuipa kwake kukadakhala ngati moto woonongeratu, ukadapsereza zinthu zanga zonse. “Ngati ndidapondereza mlandu wa mtumiki wanga, wamwamuna kapena wamkazi, pamene adabwera kwa ine ndi madandaulo ake, ndidzatani ine pamene Mulungu adzadzambatuke? Nanga akadzandifunsa, ndidzayankha chiyani? Kodi amene adapanga ine m'mimba mwa amai anga si yemwe adapanganso iyeyo? Kodi si mmodzi yemweyo amene adatilenga tonsefe? “Ngati amphaŵi ndidaŵamana zimene ankakhumba, kapena kuŵagwiritsa mwala mwankhanza akazi amasiye, ngati chakudya ndidadya ndekha, ana amasiye osachilaŵa, pakuti anawo ndidaŵalera ngati bambo wao ndi kuŵasamalira bwino chibadwire chao, ngati ndidaona wina aliyense akuzunzika ndi usiŵa, kapena munthu wosauka alibe chofunda, ngati iyeyo sadanditamande chifukwa chomupatsa chovala, ndipo ngati sindidamfunditsa ndi nsalu za ubweya wa nkhosa, ngati ndidaopsezapo mwana wamasiye, podziŵa kuti ku bwalo lamilandu sadzanditsutsa, pamenepo phewa langa lipokonyoke, mkono wanga ukonyoke m'maluma mwake. Pakutitu tsoka lochokera kwa Mulungu ndimachita nalo mantha, sindikadatha kuchita kanthu kalikonse koipa pamaso pake. “Sindidaike mtima pa chuma, kapena kudalira golide wabwino kwambiri. Zedi, sindidakondwere chifukwa choti chuma changa chinali chambiri, kapena chifukwa choti manja anga adapata zambiri. Poona dzuŵa likuŵala, kapena mwezi ukuwonetsa kukongola kwake, mtima wanga ukadakopeka nazo, dzanja langa nkuliika pakamwa mozilemekeza, bwenzi limeneli lili tchimo loti aweruzi andilange nalo, chifukwa ndikadakhala wonama kwa Mulungu wakumwamba. “Sindidakondwerere kuwonongeka kwa mdani wanga. Sindidasekere tsoka litamgwera. Sindidachimwe ndi pakamwa panga, potemberera mdani wanga kuti aonongeke. Amene ndimakhala nawo amadziŵa kuti ine ndimalandira alendo ndi kuŵapatsa chakudya chokwanira. Alendo sindidaŵasiye panja m'miseu. Aliyense wofika pakhomo panga ndidampatsa malo ogona. Anthu ena amabisa zoipa zao, koma ine sindidabise cholakwa chilichonse. Sindidaope zokambakamba za anthu kapena zonyoza za banja lina lililonse, sindidakhale chete kapena kubindikira m'nyumba chifukwa choopa iwowo. “Ha, pakadakhala wina wondimva! Ndikulumbira kuti ndikulankhula zoona. Mphambe andiyankhe. Mdani wanga akadachita kulemba pa kalata mau ake ondineneza, ndikadachita kuipachika kalatayo paphewa panga monyadira, ndikadaivalanso kumutu ngati chisoti chaufumu. Ndikadamsimbira Mulungu zonse zimene ndachita, ndikadafika pamaso pake ngati kalonga. “Ngati ndidalanda minda ya anthu ena osagula, ngati ndikulima pa minda ya eniake, ngati ndidadya zam'minda osagula, ngati ndidaphetsa eni mindayo, m'mindamo mumere minga m'malo mwa tirigu mumere namsongole m'malo mwa barele.” Mau a Yobe athera pano. Elihu adzudzula Yobe ndi abwenzi aja. Tsono anthu atatu aja adaleka osamulankhuzanso Yobe, chifukwa choti iyeyo adaadziwona kuti ndi wosachimwa. Koma Elihu, mwana wa Barakele, wa fuko la Buzi, wa banja la Ramu, adapsera mtima Yobe chifukwa chodziyesa wolungama kupambana Mulungu. Adapseranso mtima abwenzi ake atatu aja, chifukwa choti sadathe kuyankha, ngakhale iwo omwe adaapeza kuti Yobeyo ndi wolakwa. Koma Elihu adadikira kuti alankhule ndi Yobe, chifukwa choti abwenziwo anali akuluakulu kupambana iyeyo. Tsono ataona kuti anthu atatuwo sadamuyankhe Yobe moyenera, adapsa mtima. Choncho Elihu, mwana wa Barakele wa fuko la Buzi, adayamba kulankhula, adati, “Ine ndine wamng'ono, inuyo ndinu akuluakulu. Nkuwona ndinkaopa, ndipo ndinkachita mantha kuti ndikuuzeni zakukhosi. Ndinkati ayambe ndi akuluakulu aja kulankhula, chifukwa amvulazakale ndiwo amaphunzitsa nzeru. Koma mzimu wa Mphambe ndiwo umaloŵa mwa anthu ndi kuŵapatsa nzeru. Sikuti ukalamba wokha ndiwo umasandutsa anthu kuti akhale anzeru, si kukhwima kokha kumene kumachititsa kuti anthu azimvetsa zimene zili zoyenera. Nchifukwa chaketu ndikuti, ‘Mundimve, lekeni ndinenepo maganizo anga.’ “Zoona, ndinkadikira mau anuwo, ndinkafuna kumvetsera mau ogwira mtima pamene inuyo munkafunafuna zanzeru zoti mulankhule. Ndidakumvetseranidi, koma panalibe ndi mmodzi yemwe mwa inu amene adatsutsa mau a Yobe, panalibe amene adayankhako nkomwe. Chenjerani, musanene kuti, ‘Ife tapeza nzeru, Mulungu ndiye angamgonjetse, osati munthu ai.’ Yobe sadalankhule ndi ine, ndipo ine sindimuyankha monga m'mene mwamuyankhira inu.” “Iwowo asokonezeka, sakuyankhanso. Alibe ndi mau omwe oti angalankhule. Kodi ine ndidikire chifukwa iwo sakulankhula, kodi ndisayankhekonso poti iwo angoti phee? Ai, ine ndiyankhapo tsopano. Nanenso ndilankhula zakukhosi. Pakuti ndili nawo mau ambiri, mtima wanga ukundichichiza kuti ndilankhule. Ndithudi, maganizo adzaza mumtima mwanga ali ngati vinyo wopanda pompungulira, ineyo ndili ngati matumba atsopano achikopa ofuna kuphulika ndi vinyo. Ndiyenera kulankhula kuti mtima utsike. Pakufunika kuti ndiyankhepo pa nkhaniyi. Sindiwonetsa kukondera munthu wina aliyense, sindilankhula zoshashalika. Ine sindidziŵa kulankhula mochenjera, kuwopa kuti Mlengi wanga angandilange msanga.” Elihu adzudzula Yobe kuti ndi wodzikuza. “Koma tsopano inu aYobe, mverani mau anga, mutchere khutu ku zonse zimene ndinene. Tsopano ndiyamba kulankhula, ndikuuzani za mumtima mwanga. Mau anga akusonyeza kulungama kwa mtima wanga, zimene ndimazidziŵa ndimalankhula moona. Mzimu wa Mulungu udandiwumba. Mpweya wa Mphambe udandipatsa moyo. Mundiyankhe ngati mungathe. Mulankhule mau anu tsatanetsatane pamaso panga, konzekani tsono. Kunena zoona, ine ndine mnzanu pamaso pa Mulungu, poti inenso adandiwumba ndi dothi. Musachite mantha ndi kuwopsedwa nane, chifukwa sindikupanikizani koopsa ai. “Zoonadi, ndamva zimene mwalankhula, mau anu ndaŵatsata bwino. Inu mukuti, ‘Ndine woyera mtima, ndilibe cholakwa. Ndine wolungama, ndilibe tchimo. Mulungu wandipeza zifukwa zoti anditsutse nazo, Iye akundiyesa mdani wake. Akumanga mapazi anga m'zigologolo, akulonda mayendedwe anga onse.’ “Inu aYobe simukukhoza pa zimenezi, popeza kuti Mulungu ndi wamkulu kupambana munthu. Chifukwa chiyani mukulimbana ndi Mulungu nkumanena kuti, ‘Pa mau angaŵa sadzayankhapo ndi amodzi omwe?’ Pajatu Mulungu amalankhula mwa njira zosiyanasiyana, koma anthu sazindikira zimenezo. M'maloto, m'masomphenya usiku, pamene anthu ali m'tulo tofa nato, pamene akungosinza chabe pa bedi, pamenepo amaŵatsekula makutu anthuwo, naŵaopsa ndi machenjezo. Mulungu amachita izi kuti amletse munthu zoipa zimene amachita, amafuna kuthetseratu kunyada kwake. Amalanditsa munthu ku manda, amapulumutsa moyo wake kuti ungaonongeke ndi lupanga. “Mwina Mulungu amalanganso munthu ndi matenda kuti akonzeke, nthaŵiyo thupi lake lonse limangophwanya. Choncho moyo wake umanyansidwa ndi chakudya chomwe, sangadye ngakhale zakudya zabwino. Thupi lake limaonda, osatha kulithira m'maso, ndipo mafupa ake amene kale sankaoneka, amaonekera poyera. Munthuyo akutsikira ku manda, ali pafupi kupita ku malo a anthu akufa. Koma pataoneka mngelo, ngati mthandizi, mmodzi mwa ambirimbiri otere, wodzamkumbutsa zimene zili zoyenera, ngati mngeloyo amkomera mtima, nati, ‘Mpulumutseni kuti asapite ku manda, dipo lake nali,’ pamenepo thupi lake lisanduke lasee ngati lapaubwana, ndipo iye abwerere ku masiku a unyamata wake, Tsono munthu amapemphera kwa Mulungu, Iyeyo nkumulandira. Amabwera pamaso pa Mulungu mokondwa, ndipo Mulungu amamchitira zolungama. Apo adzavomera pamaso pa anthu kuti, ‘Ndidachimwa, sindidachite zolungama. Koma Mulungu sadandilange koyenerana ndi kuchimwa kwanga. Iye adandipulumutsa kuti ndisapite ku manda, ndidzaonanso kuŵala kwa dzuŵa!’ “Zoonadi, Mulungu amachita zonsezi kaŵirikaŵiri ndi anthu. Amapulumutsa moyo wa munthu ku malo a imfa, kuti athe kuwonanso kuŵala kwa moyo. “Inu aYobe, mutchere khutu, mundimvere ine. Mukhale chete, kuti ine ndilankhule. Ngati muli ndi mau, mundiyankhe. Mulankhule, chifukwa ndifuna kuti mupezeke wolungama. Ngati si choncho, mumvere ine, khalani chete, ndipo ine ndikuphunzitsani nzeru.” Mulungu ndiyedi wolungama. Elihu popitiriza kulankhula adati, “Imvani mau anga, inu anthu anzeru, mutchere khutu, inu odziŵa zinthunu. Pakuti khutu limamvetsa mau monga momwe m'kamwa mulaŵira chakudya. Tiyeni tisankhe zolungama, titsimikize tokha zimene zili zabwino. Pakuti aYobe anena kuti, ‘Ndine wosalakwa, koma Mulungu akukana kundiweruza molungama. Ngakhale ndine wolungama, akundiyesa wabodza. Mavuto anga ndi osatha, ngakhale ndine wosachimwa.’ Kodi pali munthu amene angafanefane ndi aYobe? Iwoŵa apambana kunyoza Mulungu. Amayenda ndi anthu ochita zoipa, amayanjana ndi anthu a mtima woipa. Paja ankanena kuti, ‘Palibe phindu kuti munthu azikondwerera Mulungu.’ “Tsono mumve, inu anthu anzerunu, Mulungu sangathe kuchita choipa, Mphambe sangathe kulakwa mpang'ono pomwe. Amambwezera munthu potsata ntchito zake, munthuyo zinthu zimamgwera malinga ndi mayendedwe ake. Ndithudi, Mulungu sangachite choipa, Mphambe sangaweruze mosalungama. Kodi ndani adampatsa Mulungu udindo wolamulira dziko lapansi? Ndani adaika dziko lapansi m'manja mwake? Iye akadalanda moyo wake, akadamulamula kuti mpweya wake ubwerere kwa Iye mwini, bwenzi zamoyo zonse zitaonongeka, bwenzi anthu onse atabwerera ku fumbi. “Ngati ndinu omvetsa, mumve zimenezi, mumvetsere bwino zimene ndikunenazi. Kodi munthu wodana ndi chilungamo angathe kukhala wolamulira? Kodi mungathe kumuweruza Mulungu Wolungama ndi Wamphamvu uja kuti ndi wolakwa? Mulungu amadzudzula mafumu kuti, ‘Ndinu opanda pake,’ amauza akalonga kuti, ‘Ndinu oipa.’ Iye sachita zokondera kwa akuluakulu, kapena kulemekeza olemera kupambana osauka, pakuti onsewo Mulungu adaŵalenga ndi manja ake. Iwowo amafa mwadzidzidzi, pakati pa usiku Mulungu amakantha anthu, iwowo nkufa, anthu amphamvu amaŵalanda moyo mosavuta. “Mulungu amapenya njira zonse za anthu, amaona mayendedwe ao onse. Palibe usiku kapena mdima wandiweyani kumene anthu ochita zoipa angathe kubisalira Mulungu. Mulungu sasoŵa kuchita kumuikira munthu wina aliyense nthaŵi yoti abwere pamaso pake kudzaweruzidwa. Iye amatsitsa atsogoleri, mlandu wao osaufufuza nkomwe, ndipo m'malo mwao amaikamo ena. Iyeyo amadziŵa bwino ntchito zao, amaŵagubudula usiku, iwowo nkutswanyika. Amaŵakantha chifukwa cha kuipa kwao, anthu ena onse akupenya, chifukwa adapatuka osamtsata, ndipo sankasamala malamulo ake. Adaliritsa amphaŵi kuti afuule kwa Mulungu, ndipo Iyeyo adamva kufuula kwa ovutikawo. Kodi Mulungu akangoti duu, ndani anganene kuti walakwa? Akabisa nkhope yake, ndani angathe kumpenyabe. Komabe ndiye amene amasamalira munthu kapena mtundu wa anthu, kuti asalamulidwe ndi anthu osadziŵa Mulungu, ndipo asakodwe m'misampha yao. “Kodi alipo amene adauza Mulungu kuti, ‘Ndalangika, sindidzachimwanso, mundiphunzitse zimene sindikuziwona: ngati ndidachita choipa, sindidzachitanso’? Kodi Mulungu akuweruzeni potsata m'mene inuyo mukuganizira, pamene inu mukukana kulapa? Inu ndinu amene muyenera kusankha osati ine. Nchifukwa chake munene zimene mukudziŵa. Anthu omvetsa zinthu adzandikambira, anthu anzeru amene akundimva adzandiwuza kuti, ‘Yobe akulankhula mosadziŵa, mau ake ndi opanda nzeru.’ Kunali bwino aYobe akadayesedwa mpaka ku mapeto, chifukwa choti amayankha monga m'mene amayankhira anthu oipa. Pa tchimo lao aonjezerapo upandu, akunyadira zochita zao, ndipo akuchulukitsa mau onyoza Mulungu ife tilikumva.” Mulungu amasamalira zochitika pa dziko lapansi. Elihu adaonjeza kuti, “Kodi mukuganiza kuti mukukhoza: Kunena kuti, ‘Ndine wolungama pamaso pa Mulungu?’ Kapena kufunsa kuti, ‘Kodi kuchimwa kwanga ubwino wake ndi wotani? Nanga ndikadapindulanji ndikadaleka kuchimwa?’ Ndidzakuyankhani inuyo ndi abwenzi anu omwe. Muyang'ane kumwamba, ndipo muwone mitambo imene ili kutali ndi inuyi. Kodi mukamachimwa, ndiye kuti mukumchita Mulungu chiyani? Mukamachulukitsa machimo anu, kodi mumamvuta bwanji? Kodi mukati ndinu wosalakwa, ndiye kuti mukumpindulira chiyani? Kodi angathe kulandiranji kwa inu? Kuipa kwanu kumangovuta anthu anzanu, chimodzimodzinso ntchito zanu zabwino zimangopindulira anzanu basi. “Anthu akufuula chifukwa cha kuzunzidwa. Akupempha chithandizo chifukwa anthu amphamvu akuŵavula. Koma palibe wonena kuti, ‘Kodi ali kuti Mulungu, Mlengi wanga, amene amatithandiza ngakhale pakati pa mdima wa mavuto, amenenso amatiphunzitsa kupambana nyama zam'dziko ndipo amatipatsa nzeru kupambana mbalame zouluka.’ Ena amaitana Mulungu koma Iye saŵayankha, chifukwa cha kunyada ndi kuipa kwa anthuwo. Ndithudi, Mulungu saamva kupempha kopanda pake, Mphambe sasamalako zimenezo. “Inu aYobe, mukunena kuti simungathe kupenya Mulungu, komabe mlandu wanu adzauzenga ndiye, ndipo mukudikira kuti augamule. Ndiye tsono, popeza kuti ukali wake sukupereka chilango, ndipo akuchita ngati sasamalako kwambiri zochita zoipa za anthu, inu aYobe mumangolankhula zopandapake, mukungochulukitsa mau opanda nzeru.” Ndipo Elihu adapitirira kulankhula, nati: “Mundilole pang'ono, ndipo ndikuphunzitsani. Pakuti zilipobe zoti ndinene m'malo mwa Mulungu. Nzeru zanga zikhala zochokera patali, ndiwonetsa kulungama kwa Mlengi wanga. Ndithudi, sindikunena zabodza. Wolankhula nanune ndine wanzeru kotheratu. “Zoonadi, Mulungu ndi wamphamvu, sanyoza munthu aliyense, ndipo amadziŵa zonse. Salola oipa kuti akhalebe ndi moyo, koma anthu osauka amaŵachitira zolungama. Iyeyo amatchinjiriza anthu opanda chifukwa, amalola kuti alamulire ngati mafumu, ndipo motero amalemekezeka mpaka muyaya. Koma anthu akamangidwa ndi nsinga, namazunzika chifukwa cha zimene adachita, pamenepo Mulungu amaŵasonyeza ntchito zao ndi zolakwa zao, kutsutsa kudzikuza kwao kochita kunyanya. Amaŵatsekula makutu kuti amve malangizo ake, amaŵalamula kuti asiye zoipa. Ngati anthu amumvera ndi kumamtumikira, adzatsiriza masiku a moyo wao mwamtendere, adzatsiriza zaka zao mosangalala. Koma akapanda kumvera, adzaonongeka ndi lupanga, adzafa osadziŵa kanthu. “Anthu onyoza Mulungu mumtima mwao amaputa mkwiyo wake, Mulungu akaŵalanga, iwo safuula kupempha chithandizo. Amafa akali biriŵiri, ndipo moyo wao umathera m'zonyansa. Koma Mulungu amapulumutsa ovutika mwa njira ya mazunzo ao omwe, amaŵatsekula makutu poŵagwetsa m'mavuto. Inuyo Mulungu adakutulutsaninso m'mavutowo, afuna kukuikani pabwino, osasoŵa kanthu kalikonse. “Koma tsopano inu mwapezeka opalamula ngati anthu oipa, choncho chilango cholungama cha Mulungu chakugwerani. Muchenjere kuti chuma chingakuphimbeni m'maso, musalole kuti chiphuphu chikusokezeni. Kodi kulira kwanu kungakuchotseni m'mavuto? Kodi mphamvu zanu zingakupulumutseni? Musalakelake kuti usiku ubwere, chifukwa ndiyo nthaŵi imene mitundu ya anthu idzaonongeka. Muchenjere kuti musatembenukire ku uchimo, chifukwa uchimowu ndiwo udadzetsa kuzunzika kwanu. Zoonadi, Mulungu ndi wamkulu ndiponso ndi wamphamvu. Kodi ndi mphunzitsi uti amene angafanane naye? Palibe ndi mmodzi yemwe angauze Mulungu zoti achite. Palibe aliyense amene anganene kuti ‘Mulungu ndi wolakwa.’ “Kumbukirani kutamanda ntchito za Mulungu, zimene anthu amaziyamika ndi nyimbo. Anthu onse amaona ntchitozo, koma palibe wozindikira m'mene ziliri. Ndithudi, Mulungu ndi wamkulu kwambiri, sitimdziŵa mpang'ono pomwe. Chiŵerengero cha zaka zake nchosadziŵika. Mulungu ndiye amakweza timadontho ta madzi ku thambo kuchokera pansi, ndipo amasungunula mitambo kuti ikhale mvula. Mitambo imatsanyula mvulayo, ndipo mvulayo imavumba pa anthu mokwanira. Kodi alipo wina woti angadziŵe kuyenda kwa mitambo kapena kugunda kwa zing'aning'ani? Mulungu amaŵalitsa zing'aning'ani kuthambo kwake konse, zimafika ngakhale pansi pa nyanja. Mulungu amachenjeza mitundu ya anthu podzera m'zimenezi, komabe amapereka chakudya chochuluka. Amagwira zing'aning'ani, ndipo amazilamula kuti zigwe pa malo amene Iye akufuna. Kugunda kwake kumalengeza kuti Iye alipo, ndiye amalanga uchimo mwaukali. Nanenso ndimaopa zazikuluzi, mtima wanga umalumphalumpha kuchoka m'malo mwake. Mumvetsetse kulira kwa liwu la Mulungu, ndiye kuti kugunda kotuluka m'kamwa mwake. Amaponya ching'aning'ani pansi pa thambo, kuŵala kwake kumafika ku ngodya zonse za dziko lapansi. Pambuyo pake kugunda kwa Mulungu kumamveka, amagunda ndi liwu lake lalikulu pamene mphezi zikung'anipa. Mulungu amachita zodabwitsa ndi liwu lake. Amachita zazikulu zimene sitingathe kumvetsa. Amalamula chisanu chambee kuti chigwe pa dziko lapansi. Amalamulanso mvula kuti igwe mwamphamvu. Pamenepo Mulungu amalepheretsa anthu kugwira ntchito zao. Motero iwowo amazindikira kuti Iye mwini ali pa ntchito. Pomwepo zilombo zimathaŵira ku michembo yake, ndipo zimakabisalira m'ngaka zake. Kamvulumvulu amakuntha kuchokera ku malo ake, mphepo imadzetsa chisanu chambiri. Mpweya wa Mulungu umaunditsa chisanu, ndipo madzi am'nyanja amauma kuti gwa. Mitambo yochindikira amaidzaza ndi madzi a mvula, ndipo amabalalitsa zing'aning'ani kuchokera m'mitambo. Mulungu amayendetsa mitambo mozungulirazungulira, kuti ichite zonse zimene Iye akufuna pa dziko lapansi. Mwina amagwetsa mvula pansi pano kuti ikhale chilango, mwina kuti aonetse chikondi kwa anthu, pothirira nthaka yao. “Inu aYobe, tamvani izi, imani, muganizire ntchito zodabwitsa za Mulungu. Kodi mukudziŵa m'mene Mulungu amazichitira, ndi m'mene amang'anipitsira mphezi m'mitambo yake? Kaya mukudziŵa m'mene Mulungu amayalira mitambo, ntchito yosonyeza nzeru zake zodabwitsa, paja inu zovala zanu mumamva kutentha kwambiri pamene mphepo yakumwera ikuwomba pa dziko? Kodi mungathe kufanafana naye Mulungu amene adatambasula thambo lili lolimba ngati chitsulo? “Chabwino, tiphunzitsenitu zoti tidzamuuze. Ifeyo sitingathe kunena kanthu poti mwa ife mwachita mdima. Kodi nkofunikira kumdziŵitsa Mulungu kuti ndili naye ndi mau? Kodi kutero si kuchita ngati kupempha kuti ndiwonongeke? “Tsopano anthu sangathe kuyang'anitsitsa kuŵala, pamene kukunyezimira kwambiri mu mlengalenga, pamene mphepo yaomba nkuchotsa mitambo yonse. Kuŵala kwake kumaonekera chakumpoto. Mulungu amaonetsa ulemerero woopsa. Mphambe sitingathe kumufika pafupi, ndi woopsa pa ulamuliro ndi pa mphamvu. Ndi wolungamadi kwambiri, sangazunze anthu. Nchifukwa chake anthu amamuwopa kwambiri. Iye sasamalako wina aliyense amene amadzinyenga kuti ndi wanzeru.” Chauta alankhula. Apo Chauta adayankha Yobe m'kamvulumvulu kuti, “Kodi ndiwe amene ukusokoneza uphungu wanga polankhula mau opanda nzeru? Onetsa chamuna, ndidzakufunsa, ndipo undiyankhe. “Kodi udaali kuti pamene ndinkaika maziko a dziko lapansi? Undiwuze ngati ndiwe womvetsa zinthu. Nanga kodi ukudziŵa amene adalemba malire ake, amene adayesapo ndi chingwe padzikopo? Kodi maziko ake adaŵakumba potani? Nanga mwala wake wapangodya adauika ndani? Pa nthaŵiyo nyenyezi zakuvuma zinkaimba pamodzi, ndipo angelo onse a Mulungu ankafuula mokondwa? “Kodi ndani amene adatsekera nyanja pamene inkalengedwa pamene inkachita ngati kutumphuka pansi pa dziko? Ndinetu amene ndidakuta nyanjayo ndi mitambo, ndidaiveka mdima ngati chovala. Ndidailembera malire, ndidaiikira mipiringidzo ndi zitseko zake. Tsono ndidati, ‘Ufike mpaka apo osabzolapo, mafunde ako amphamvuwo aime pomwepo.’ “Kodi chibadwire chako udalamulapo dzuŵa kuti lituluke m'maŵa, ndi kuti mbandakucha ukhalepo pa nthaŵi yake? Kodi iweyo udalamulapo kuti kuŵala kwa mbandakuchawo kuunikire dziko lonse lapansi, kuti kuthaŵitse anthu oipa obisala pamenepo? Chifukwa cha kuŵala kwa usana mapiri ndi zigwa zimaonekera bwino ngati makwinya a chovala ngati zilembo za chidindo pa mtapo. Kuŵala kwa dzuŵa sikuŵafika anthu oipa, choncho sangathe kugwira ntchito zao. “Kodi udakayendapo pansi penipeni pa nyanja ndi kukafika pa magwero ake? Kodi adakuwonetsa iwe zipata za imfa? Kodi udaonako ku dziko la anthu akufa kumene kuli mdima wokhawokha? Kodi kukula kwa dziko lapansi umakudziŵa? Undiwuze tsono ngati umazidziŵa zonsezi. “Kodi njira yopita kumene kumakhala kuŵala ili kuti? Nanga mdima, kwao nkuti? Kodi iwe ungathe kuziperekeza kwaoko zimenezi, kodi ukuidziŵa njira yopita kwaoko? Makamaka ukudziŵadi ati, poti paja nthaŵi imeneyo nkuti iweyo utabadwa, ndipo zaka zako kuchuluka ati! “Kodi udaloŵamo m'nyumba zosungiramo chisanu, kapena m'mene amasungira matalala? Zimenezi ndazisungira nthaŵi ya mavuto, ndidzazitumiza nthaŵi yomenyana nkhondo. Kodi udapitako kumene kumatulukira dzuŵa, kapena kumene kumachokera mphepo yakuvuma? “Kodi ndani amene adakonza ngalande za mvula? Ndani adakonza njira zodzeramo mphezi? Ndani amagwetsa mvula pa chipululu popanda anthu, ku dziko kumene sikukhala anthu. Ndani amathirira dziko louma lagwaa, kotero kuti udzu umamerapo? “Kodi mvula ili ndi bambo wake? Nanga madzi a mame adaŵabeleka ndani? Kodi chisanu choundana adachibala ndani? Nanga adabereka chipale chochokera kumwamba ndani? Ndani amasandutsa madzi kuti alimbe ngati mwala, pamene madzi apanyanja amazizira, nalimba kuti gwaa? “Kodi Nsangwe iwe ungazimange maunyolo? Kodi zingwe za Akamwiniatsatana iwe ungathe kuzimasula? Kodi ungathe kuwongolera nyenyezi pa nyengo yake? Kodi ungathe kutsogolera nyenyezi yaikulu ya Chimbalangondo pamodzi ndi tiana take? Kodi malamulo a mlengalenga umaŵadziŵa? Nanga ulamuliro wake, kodi ungaukhazikitse pa dziko lapansi? “Kodi iwe ungathe kulamula mitambo kuti igwetse mvula ya chigumula? Kodi ungathe kutumiza zing'aning'ani kuti zing'anipe, ndi kugwera pa malo amene iwe ukufuna? Ndani amene adayala mitambo bwino mu mlengalenga? Nanga ndani adalangiza mvula kuti igwere pakutipakuti? Wanzeru ndani amene angathe kuŵerenga mitambo, nanga ndani angathe kupendeketsa mitsuko ya madzi akuthambo amene amasandutsa fumbi matope, ndi kuumba zibumi? “Kodi iwe ungathe kuufunira chakudya mkango? Kodi ungathe kuipatsa chakudya misona yake ija, pamene ili khale m'mapanga mwake, kapena pamene ikubisala m'tchire? Kodi khwangwala amampatsa chakudya chake ndani, pamene maunda ake akulirira kwa Mulungu, namadzandira chifukwa chosoŵa chakudya?” “Kodi iwe umaidziŵa nthaŵi imene zinkhoma zimaswera? Kodi udaziwonapo nswala zikubadwa? Kodi ungathe kuŵerenga miyezi imene zimakhala ndi bele? Kodi nthaŵi imene nyamazi zimaswa iwe umaidziŵa? Kodi ukuidziŵa nthaŵi imene zidzakhala tsonga nkuswa ana, kenaka nkutayiza? Ana a nyamazi amakhala amphamvu, namakulira ku thengo. Pambuyo pake amapita, osabwereranso kwa mai wao. “Kodi abulu akuthengo adaŵapatsa ndani ufulu wongodziyendera? Ndani adaŵapatsa liŵilo lao? Ine ndidaŵapatsa chipululu kuti chikhale malo ao okhalako, ndiponso chichere kuti chikhale dera lao. Amakhala kutali ndi mizinda yaphokoso, ndipo sadziŵa mau okuwa a anthu oyendetsa nyama zakatundu. Kumapiri ndiko kumene kuli busa lao. Kumene amafunafuna msipu woti adye. “Kodi njati ingavomere kukutumikira? Kodi ingagone m'khola mwako usiku? Kodi ungathe kuimanga ndi nsinga kuti izilima? Kodi ingasalaze nthumbira m'munda mwako? Kodi ungadalire njatiyo chifukwa cha mphamvu zake? Kodi ungayembekeze kuti ikugwirira ntchito yako? Kodi ungakhulupirire kuti idzabwera nkudzatuta tirigu wako ku malo opunthira? “Nthiŵatiŵa ikukupiza mapiko ake monyadira, koma nthenga zake ndi mapiko ake sizikuithandiza kuuluka monga amachitira kakoŵa. Nthiŵatiŵa imafotsera mazira ake pansi, kuti afundidwe m'nthaka. Koma imaiŵala kuti mapazi ake omwe angathe kuphwanya mazirawo, ndipo kuti nyama zakuthengo nkuŵapondereza. Nthiŵatiŵa imachita ana ake nkhalwe ngati si ake. Zakuti idaavutika poŵabereka imaiŵalako. Paja Mulungu adaimana nzeru, kotero kuti simvetsa kanthu kalikonse. Komabe nthiŵatiŵayo ikadzambatuka nkuyamba kuthaŵa, imamsiya kutali kavalo ndi wokwerapo wake. “Kodi ndiwe amene umapatsa mphamvu kavalo? Nanga ndiwe amene umaveka chenjerere m'khosi mwake? Kodi ndiwe amene umamlumphitsa ngati dzombe? Kavalo akamadzuma, mpweya wake ndi waukali ndiponso woopsa. Kavaloyo amalumphalumpha m'chigwa, ndipo amapita ku nkhondo ndi mphamvu zake zonse. Sachita mantha, sachita nkhaŵa, ndipo sabwerera m'mbuyo akaona lupanga. Zida zankhondo za wokwerapo wake zimachita kwichikwichi m'phodo, ndipo mkondo ndi nthungo zimanyezemira pa dzuŵa. Akavalowo amanjenjemera ndi ukali nathamangira kutsogolo, ndipo akangomva lipenga sangathe kuima. Lipenga likalira amati, ‘Twee!’ Amamva fungo la nkhondo ali patali. Amamva kufuula kwa atsogoleri ankhondo. “Kodi ndi nzeru zako zimene zimaphunzitsa kabaŵi kuuluka, ndi kutambalitsa mapiko ake kupita chakumwera? Kodi umalamula chiwombankhanga ndiwe kuti chiziwuluka? Kodi udachiphunzitsa ndiwe kukamanga chisa pamwamba penipeni? Chimakhala pa phiri, nkumanga chisa chake pamenepo, pansonga penipeni pa thanthwe losakwereka. Pamenepo chimayang'ana choti chigwire kuti chidye, ndipo maso ake amachiwonera patali chinthucho. Ana ake amayamwa magazi, amapezeka kumene kuli mitembo.” Kuyankha kwa Yobe. Tsono Chauta adafunsa Yobe kuti, “Kodi munthu wamakaniwe ufuna kukangana ndi Mphambe? Chabwino, iwe amene unatsutsana ndi Mulungu uyankhe zimenezo.” Apo Yobe adayankha Chauta kuti, “Ine sindili kanthu konse! Kodi ndingathe kukuyankhani chiyani? Palibe, koma kungogwira pakamwa. Ndidalankhula kamodzi, sindiyankhanso. Ndidalankhula kaŵiri, sindiwonjezanso kanthu kena.” Mau a Chauta. Tsono Chauta adayankha Yobe m'kamvulumvulu kuti, “Tsopano vala dzilimbe ngati mphongo. Ndikufunsa mafunso, iweyo undiyankhe. Kodi ungandiyese ine wolakwa? Kodi ungandidzudzule kuti iweyo ukhale wolungama? Kodi uli ndi mphamvu monga Ine Mulungu? Kodi mau ako angagunde monga m'mene amagundira mau anga? “Ngati zili choncho udzipatse ufumu ndiponso ulemu. Uvale ulemerero wachifumu. Tsanyula mkwiyo wako wosefukira, uyang'ane aliyense wodzikuza, ndipo umchepetse. Uyang'ane aliyense wodzikweza, ndipo umtsitse. Oipa onse uŵaponderezere pamalo pomwe aliripo. Onsewo uŵafwirise pamodzi m'chifwilimbwiti. Uŵakulunge kumaso m'dziko la anthu akufa. Ukatero, nanenso ndidzakuvomereza, kuti mphamvu zako zakupambanitsadi. “Taganiza za mvuu, Ine ndidaipanga monga momwe ndidapangira iwe. Imadya udzu ngati ng'ombe. Mphamvu zake ndi zazikulu kwambiri, thupi lake ndi lanyonga zedi. Imaimiritsa mchira wake kuti tototo, ngati mtengo wa mkungudza. Mitsempha ya ntchafu zake ndi yogwirana bwino. Mafupa ake ndi olimba ngati misiwe yamkuŵa, nthiti zake zili ngati mipiringidzo yachitsulo. “Mvuu ndiyo yaikulu mwa zolengedwa za Ine Mulungu. Ine amene ndidailenga ndidaipatsa maso ake oopsa aja. Imapeza chakudya kumtunda kumene nyama zonse zakuthengo zimaseŵera. Imagona patsinde pa zitsamba za mipeta, imabisalika m'bango ndiponso pa thaŵale. Zitsamba za mipeta ndizo zimaipatsa mthunzi. Misondodzi yamumtsinje imaiphimba. Madzi amumtsinje akamakokoma, iyo sichita mantha. Ngakhale madzi a mu Yordani aiyese m'khosi, sitekeseka nazo. Kodi nanga alipo wina amene angathe kukola mvuu ndi mbedza kapena kuikola mu msampha? Kodi ungathe kuchikoka ndi mbedza ya nsomba chilombo chija cha Leviyatani, kapena kukanikiza lilime lake pansi ndi chingwe? Kodi ungathe kuchimanga chingwe m'mphuno mwake, kapena kuchiboola nsagwada ndi mbedza? Kodi chidzakupempha kuti uchimasule? Kodi chidzakupemba kuti uchichitire chifundo? Kodi chidzachita nawe chipangano kuti chikhale chokutumikira mpaka muyaya? Kodi ungaseŵere nacho ngati mbalame? Kodi kapena nkuchimanga ndi unyolo kuti adzakazi ako aseŵere nacho? Kodi asodzi nkuchitsatsa malonda? Nanga amalondawo nkugaŵanagaŵana nyama yake kuti akaigulitse? Kodi chikopa chake ungathe kuchilasa ndi ntcheto, kapena kuboola mutu wake ndi nthungo zophera nsomba? Ukachiputa, udziŵe kuti pali nkhondo, ndipo iweyo sudzabwereranso. Ndithu, aliyense akachiwona chilombocho, amataya mtima, ndipo amangodzigwera ndi mantha. Ngati palibe wina woti angalimbe mtima nkuchiputa. Nanga ndani angalimbe mtima nkukangana ndi Ine Mulungu? Kodi ndani adandipatsa kanthu, kuti Ineyo ndimbwezere? Zonse za pansi pa thambo ndi zanga. “Sindingaleke kulankhula za ziwalo zake za chilombocho, za mphamvu zake ngakhalenso za maonekedwe a thupi lake. Ndani angasende chikopa chake? Ndani angachibaye chikopa chimene chija, kulimba konse kuja ngati chovala chachitsulo? Ndani angatsekule kukamwa kwake? Mano ake ndi oopsa. Kumsana kwake kuli mizere ya mamba onga zishango zolumikizanalumikizana, onse olimba ngati mwala. Mambawo ndi olukanalukana, kotero kuti ndi mpweya womwe sungathe kuloŵa pakati pake. Ndi olumikizanalumikizana, ndi omamatirana kwambiri, kotero kuti sangathe kutayana. Kuyetsemula kwake kumatulutsa mbaliwali, maso ake amaŵala ngati kuŵala kwa mbandakucha. M'kamwa mwake mumatuluka nsakali za moto, mumathetheka mbaliwali za moto. M'mphuno mwake mumatuluka utsi, ngati wa m'nkhali yogaduka ndiponso ngati wa moto wa mlulu. Mpweya wake umayatsa makala, malaŵi a moto amatuluka m'kamwa mwake. Khosi lake ndi lamphamvu kwambiri, aliyense wokumana nacho amangoti njenjenje ndi mantha. Minyewa ya thupi lake ndi yolumikizana, ndi yokhwima kwambiri, ndipo ndi yolimba. Pachifuwa pake mpouma ngati mwala. Pali gwa! Ngati mwala wa mphero. Chilombocho chikangoti vuuku, ndi amphamvu omwe amaopa. Akamva phokoso lake, amachita mantha. Ngakhale lupanga lichikanthe, silichichita kanthu. Mkondo, muvi ndi nthungo, zonse zimalephera. Chitsulo chimachiyesa phesi chabe, mkuŵa chimauyesa chikuni choola. Muvi sungathe kuchithaŵitsa, Miyala imene achilasa nayo, chimangoinyenyanyenya. Zibonga zimakhala ngati ziputu. Akamachitchaya ndi nthungo, icho chimangoseka. Za kumimba kwake zili ngati mapale akuthwa. Chimatambalala m'matope ngati galeta lopunthira tirigu. Chimagadutsa madzi ozama ngati madzi am'nkhali, chimasandutsa nyanja kuti igaduke ngati mbiya yoyengeramo mafuta. Kumbuyo kwake chimasiya nthubwitubwi zambee, kotero kuti munthu angaganize kuti nyanja yachita imvi. Pa dziko lapansi palibe china chofanana nacho, ncholengedwa chopanda mantha. Chimanyoza nyama zina zonse. Icho chija ndi mfumu ya nyama zonse.” Mau omaliza a Yobe. Tsono Yobe adayankha Chauta kuti, “Ndikudziŵa kuti Inu mungathe kuchita zinthu zonse, chimene mufuna kuchita, wina sangaletse konse. Munandifunsa bwino kuti, ‘Kodi ndiwe yani amene ufuna kusokoneza uphungu wanga ndi mau opanda nzeru?’ Zoonadi ndidalankhula zimene sindidazidziŵe, zinthu zodabwitsa kwa ine zimene sindidazimvetse konse. Munandiwuza kuti, ‘Umvetsetse ndipo ndidzalankhula. Ndidzakufunsa, ndipo iweyo undiyankhe.’ Ndinkangomva za inu ndi makutu, koma tsopano ndakuwonani chamaso. Nchifukwa chake ndikuchita manyazi ndi zonse zimene ndidakamba, ndikulapa podzithira fumbi ndi phulusa.” Mulungu adalitsanso Yobe. Chauta atalankhula ndi Yobe mau ameneŵa, adauza Elifazi wa ku Temani kuti, “Ine ndakukwiyira kwambiri pamodzi ndi abwenzi ako aŵiri, chifukwa simudalankhule zabwino za Ine, monga m'mene walankhulira mtumiki wanga Yobe. Nchifukwa chake tsopano mutenge ng'ombe zamphongo zisanu ndi ziŵiri ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziŵiri, mupite nazo kwa mtumiki wanga Yobe, mukaperekere nsembe zopsereza. Tsono mtumiki wangayo adzakupemphererani, pakuti pemphero lakelo ndidzalilandira kuti ndisakuchiteni kanthu potsata kupusa kwanu. Inu simudalankhule zabwino za Ine, monga adalankhulira Yobe mtumiki wanga.” Motero Elifazi wa ku Temani, Bilidadi wa ku Suki ndi Zofari wa ku Naama adapita, nakachita zimene Chauta adaŵauza. Ndipo Chauta adamveradi pemphero la Yobe. Choncho Yobe ataŵapempherera abwenzi ake aja, Chauta adambwezera chuma chake. Adampatsa moŵirikiza kuposa zimene adaali nazo kale. Tsono abale ake onse ndi alongo ake omwe, kuphatikizapo onse amene ankamdziŵa kale, adabwera kwa iye nkudzadya naye chakudya m'nyumba mwake. Choncho adampepesa, namuthuzitsa mtima chifukwa cha mavuto onse amene Chauta adaalola kuti amgwere. Tsono aliyense mwa iwowo adampatsa ndalama ndi mphete yagolide. Motero Chauta adadalitsa Yobe pa masiku ake otsirizaŵa kupambana poyamba paja. Tsono adakhala ndi nkhosa 14,000, ngamira 6,000, ng'ombe 2,000, ndi abulu aakazi 1,000. Adabalanso ana aamuna asanu ndi aŵiri ndi ana aakazi atatu. Wamkulu mwa ana aakazi aja adamutcha Yemima. Wachiŵiri anali Keziya, wachitatu anali Kerehapuki. M'dziko monsemo munalibe akazi okongola ngati ana a Yobe. Bambo wao adaŵapatsa choloŵa chimodzimodzi ngati alongo ao. Pambuyo pake Yobe adakhala ndi moyo zaka 140. Tsono adaona ana ake ndi zidzukulu zake mpaka mbadwo wachinai. Potsiriza Yobe adamwalira, ali nkhalamba ya masiku ochuluka zedi. Ngwodala munthu wosatsata uphungu wa anthu oipa, wosatsanzira mayendedwe a anthu ochimwa, wosakhala nawo m'gulu la anthu onyoza Mulungu, koma wokondwerera kumvera malamulo a Chauta, nkumasinkhasinkha za malamulowo usana ndi usiku. Munthuyo ali ngati mtengo wobzalidwa m'mbali mwa mtsinje wa madzi, ngati mtengo wobereka zipatso pa nthaŵi yake, umene masamba ake safota konse. Zochita zake zonse zimamuyendera bwino. Anthu oipa sali choncho, ali ngati mungu wouluzika ndi mphepo. Nchifukwa chake anthu ochimwa, Mulungu adzaŵazenga mlandu, adzaŵachotsa iwo pakati pa anthu ake. Paja Chauta amaŵasamalira anthu ake, koma anthu ochimwa adzaonongeka. Bwanji anthu akunja akufuna kuchita chiwembu? Chifukwa chiyani anthu ameneŵa akulingalira zopandapake? Mafumu ao akuchita upo, olamula ao akhala pamodzi kuti apangane zoipa, zoukira Chauta ndi mfumu yake yodzozedwa. Akuti, “Tiyeni timasule maunyolo aoŵa, tichokeretu mu ulamuliro wao.” Chauta amene amalamulira kumwambako akungoŵaseka ndi kuŵanyoza. Tsono adzaŵadzudzula ali wokwiya adzaŵaopseza ali wokalipa. Adzati, “Ine ndakhazika kale mfumu yanga, ili pa phiri langa loyera la Ziyoni.” Tsono mfumuyo ikuti, “Ndidzalalika zimene Chauta walengeza. Adandiwuza kuti, ‘Iwe ndiwe mwana wanga, Ine lero ndakubala. Tandipempha uwone, ndidzasandutsadi mitundu ya anthu kuti ikhale choloŵa chako, ndipo dziko lonse lapansi lidzakhala lako. Udzaŵaphwanya ndi ndodo yachitsulo, ndi kuŵatekedza zidutswazidutswa monga mbiya.’ ” Nchifukwa chake tsono khalani anzeru, inu mafumu. Chenjerani inu amene muli olamula dziko lapansi. Tumikirani Chauta mwamantha ndi monjenjemera. Mumgonjere molapa, kuwopa kuti angakukwiyireni, ndipo inu mungaonongeke, chifukwa ukali wake umayaka msanga. Ngodala onse amene amathaŵira kwa Iye. Inu Chauta, ndili ndi adani ochuluka, anthu ambiri akundiwukira. Anthu ambiri akamalankhula za ine amati, “Mulungu samupulumutsa.” Koma Inu Chauta, ndinu chishango changa chonditeteza, ndinu ulemerero wanga, mumalimbitsa mtima wanga ndinu. Ndimafuulira Chauta kuti andithandize, Iye amandiyankha ali pa phiri lake loyera. Ndimagona ndipo ndimapeza tulo. Ndimadzukanso m'maŵa pakuti Chauta amanditchinjiriza. Sindichita mantha ngakhale adani anga ndi osaŵerengeka, ngakhale andizinge ndi kundithira nkhondo. Inu Chauta, dzambatukani, mundipulumutse Inu Mulungu wanga. Adani anga onse mwaŵaomba makofi, anthu oipa mwaŵagulula mano. Mumatipulumutsa ndinu, Inu Chauta. Madalitso anu akhale pa anthu anu. Ndikamaitana, mundiyankhe Inu Mulungu, Mtetezi wanga. Mudabwera kudzandithandiza pamene ndinali m'mavuto. Mundichitire chifundo, ndi kumvera pemphero langa. Anthu inu, mudzaleka liti kunyoza ulemu wanga? Bwanji mukukondabe zinthu zachabechabe? Bwanji mukulakalakabe zinthu zonama? Koma tsono mudziŵe kuti Chauta wadzipatulira Iye yemwe anthu olungama. Chauta amamva ndikamuitana. Opani Mulungu, ndipo musachimwe. Mukhale phee ndipo muganize zimenezi mu mtima pamene mukugona. Perekani nsembe zanu ndi mtima wolungama, ikani mitima yanu pa Chauta. Alipo ambiri amene amati, “Ndani angatiwonetse zabwino? Mutiyang'ane ndi chikondi chanu, Inu Chauta.” Koma Inu mwandisangalatsa mtima kwambiri, kupambana anthu a zakudya ndi zakumwa zambiri! Choncho ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere, pakuti Inu nokha Chauta ndinu amene mumandisunga bwino lomwe. Imvani mau anga, Inu Chauta, mverani kusisima kwanga. Imvani kulira kwanga, Inu Mfumu yanga ndi Mulungu wanga, pakuti ndikupempha chithandizo kwa Inu. M'maŵa, Inu Chauta, mumamva mau anga. M'maŵa ndimapemphera kwa Inu, ndi kudikira kuti mundiyankhe. Inu sindinu Mulungu wokondwerera machimo. Simufuna zoipa pamaso panu. Anthu onyada sangathe kuwonekera pamaso panu. Inu mumadana ndi anthu onse ochita zoipa. Inu mumaŵaononga anthu olankhula zonama. Inu Chauta mumanyansidwa nawo anthu onyenga ndi opha anzao. Koma ine ndidzatha kuloŵa m'Nyumba mwanu chifukwa cha kukula kwa chikondi chanu. Ndidzaŵeramitsa mutu pansi, kupembedza Inu m'Nyumba yanu yoyera. Inu Chauta, ndinu olungama, munditsogolere pakati pa adani ondizonda. Mundikonzere njira yoongoka kuti ndidzeremo. Adani anga amalankhula mabodza okhaokha. Mtima wao umangofuna kuwononga. Mummero mwao muli ngati manda apululu, ndipo lilime lao limalankhula zonyenga. Asenzetseni tchimo lao, Inu Mulungu. Upo wao woipa uŵagwetse iwo omwe, muŵachotse pamaso panu chifukwa cha zochimwa zao zambirimbiri, chifukwa akuukirani Inu. Koma onse othaŵira kwa Inu akondwere, aziimba ndi chimwemwe nthaŵi zonse. Inu muŵatchinjirize, kuti okukondani akondwere chifukwa cha chitetezo chanu. Inu Chauta, mumadalitsa munthu wochita chilungamo. Kukoma mtima kwanu kuli ngati chishango chomuteteza. Inu Chauta, musandikalipire ndi kundidzudzula, musapse mtima ndi kundilanga. Ndichitireni chifundo, Inu Chauta, chifukwa chakuti ndine wofooka. Limbitseni, Inu Chauta, chifukwa m'nkhongono mwanga mwaweyeseka. Mtima wanganso wazunzika kwambiri. Nanga Inu Chauta, zimenezi zidzakhala zikuchitika mpaka liti? Bwerani, Inu Chauta, mudzandilanditse. Mundipulumutse chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika. Anthu akufa sangathe kukutamandani ku manda. M'dziko la akufa ndani angathe kukuyamikani? Ndatopa nkubuula kwambiri. Ndimanyowetsa bedi langa ndi misozi usiku uliwonse. Ndimakhathamiza pogona panga chifukwa cha kulira kwanga. Maso anga atupa chifukwa cha kulira, afooka chifukwa cha adani anga onse. Chokani apa, inu nonse ochita zoipa, Chauta wamva kulira kwanga. Chauta wamva pemphero langa ndipo wandiyankha. Adani anga onse adzagonjetsedwa mwa manyazi ndipo adzagwidwa ndi mantha, modzidzimuka onse adzathaŵa motaya mtima. Chauta, Mulungu wanga, ndikuthaŵira kwa Inu. Mundilanditse kwa onse ondithamangitsa. Mundipulumutse, kuti iwo anganding'ambe ngati mkango, ndi kundikadzula popanda wina wondipulumutsa. Chauta Mulungu wanga, ngati ndachita izi: kumchimwira munthu aliyense, kubwezera choipa bwenzi langa, kapena kumulanda zinthu mdani wanga popanda chifukwa, mdaniyo andithamangitse ndi kundigwira, andipondereze pansi ndi kundipha, andisiye ndili thasa m'fumbi. Nyamukani, Inu Chauta, muli okwiya, mulimbane ndi adani anga aukali. Dzambatukani, Inu Mulungu wanga, amene mwalamula kuti chilungamo chichitike. Musonkhanitse anthu a mitundu yonse pafupi ndi Inu, ndipo muŵaweruze mutakhala pa mpando wanu kumwamba. Chauta amagamula milandu ya anthu. Tsono thetsani mlandu, Inu Chauta, moyenera, popeza kuti ine sindidalakwe konse. Thetsani ntchito zoipa za anthu ochimwa, koma anthu ochita zabwino muŵabwezere zokoma. Inu ndinu amene mumayesa maganizo ndi mitima yomwe, Inu ndinu Mulungu wolungama. Mulungu ndiye chishango changa, amapulumutsa anthu olungama mtima. Mulungu ndiye muweruzi wolungama, amalanga anthu oipa nthaŵi zonse. Ngati munthu salapa, Mulungu adzanola lupanga lake, adzakunga ndi kukoka uta wake. Wakonza zida zake zoopsa, waika mivi yamoto ku uta wake. Zoonadi, munthu woipa amalingalira zoipa zokhazokha nthaŵi zonse, ntchito yake ndi kunyenga ndi kuvutitsa anthu ena basi. Amakumba mbuna kuti ikhale yozama, koma amagwamo ndiye yemwe. Choipa chitsata mwini, chiwawa chimabwerera pa mwini wake. Ine ndidzathokoza Chauta chifukwa cha kulungama kwake, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina la Chauta, Wopambanazonse uja. Chauta, Ambuye athu, dzina lanu ndi lotchuka pa dziko lonse lapansi. Kumwamba amaimba nyimbo zotamanda ulemerero wanu. Nawonso ana ndi makanda omwe amauimbira. Mwamanga linga chifukwa cha adani anu, kuti mugonjetse onse okuukirani. Ndikamayang'ana ku thambo lanu limene mudapanga ndi manja anu, ndikamaona mwezi ndi nyenyezi zimene mudazikhazika kumeneko, ndimadzifunsa kuti, “Kodi munthu nchiyani kuti muzimkumbukira, mwana wa munthu nchiyani kuti muzimsamalira?” Ndiyetu mudamlenga mochepera pang'ono kwa Mulungu amene, mudampatsa ulemerero ndi ulemu wachifumu. Mudampatsa ulamuliro pa ntchito za manja anu. Mudamgonjetsera zolengedwa zonse, nkhosa, ng'ombe ndi nyama zakuthengo, mbalame zamumlengalenga, nsomba zam'nyanja, ndi zonse zoyenda pansi pa nyanja. Chauta, Ambuye athu, dzina lanu ndi lotchuka pa dziko lonse lapansi. Ndidzakuthokozani, Inu Chauta, ndi mtima wanga wonse. Ndidzasimba za ntchito zanu zonse zodabwitsa. Ndidzakondwa ndi kusangalala chifukwa cha Inu, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu, Inu Wopambanazonse. Mukangofika, adani anga amathaŵa, amaphunthwa ndi kufa pamaso panu. Inu mwatsimikiza kusalakwa kwanga. Mwakhala pa mpando woweruza, mwagamula kuti ndine wosapalamula. Mwaimba mlandu mafuko a anthu, mwaononga anthu oipa. Adzaiŵalika mpaka muyaya. Adani athu atha phu. Mwapasula mizinda yao kotheratu, anthu sadzaikumbukiranso. Koma Chauta amakhala pa mpando wake waufumu nthaŵi zonse, adakhazika mpando wake kuti aziweruza. Iye amaweruza dziko lapansi molungama, amagamula milandu ya anthu mosakondera. Kwa Chauta ndiye kothaŵirako anthu opsinjidwa, ndiyenso kopulumukira pa nthaŵi yamavuto. Amene amadziŵa dzina lanu, Inu Chauta, amakukhulupirirani, pakuti Inu Chauta simuŵasiya anthu okufunitsitsani. Imbani nyimbo zotamanda Chauta amene amakhala ku Ziyoni. Lalikani za ntchito zake kwa anthu a mitundu yonse. Paja Iye amachitira chifundo anthu ozunzika, salephera kumva kulira kwao ndipo amalanga anthu oŵazunzawo. Mundikomere mtima, Inu Chauta. Onani m'mene akundisautsira anthu ondida. Inu mumandipulumutsa ku imfa, kuti ndithe kuyamika ntchito zanu zonse, pakati pa anthu anu a mu Ziyoni. Zoonadi ndidzakondwa chifukwa mwandipulumutsa. Akunja agwera m'mbuna yokumba iwo omwe. Phazi lao lakodwa mu ukonde wobisika wotcha iwo omwe. Chauta wadziwulula yekha, pakuweruza molungama, koma anthu oipa akodwa mu msampha wotcha iwo omwe. Tsono anthu oipa adzapita ku dziko la anthu akufa, ndiye kuti anthu onse amene amakana Mulungu. Koma anthu aumphaŵi Mulungu saŵaiŵala nthaŵi zonse, anthu osauka Mulungu saŵagwiritsa mwala mpang'ono pomwe. Dzambatukani, Inu Chauta, munthu asakunyozeni. Azengeni mlandu anthu akunja. Inu Chauta, aopseni anthuwo. Akunjawo adziŵe kuti iwo ndi anthu chabe. Chifukwa chiyani mumaima kutali nafe, Inu Chauta? Chifukwa chiyani mumabisala pamene tili pa mavuto? Anthu oipa amazunza anthu osauka modzikuza. Akodwe m'misampha yotcha iwo omwe. Paja munthu woipa amanyadira zokhumba za mtima wake, wokonda chuma amanyoza ndi kukana Chauta. Munthu woipa sasamala Mulungu chifukwa cha kunyada kwake. Mumtima mwake amati, “Kulibe Mulungu.” Zinthu zimamuyendera bwino nthaŵi zonse. Chiweruzo chanu chili naye kutali, ndipo salabadako konse. Kunena za adani ake, iye amangoŵanyodola. Mumtima mwake amaganiza kuti, “Sindidzagwedezeka, sindidzaona konse mavuto.” Pakamwa pake pamangolankhula zotemberera, zonyenga ndi zoopseza. M'kamwa mwake mumatuluka zovutitsa ena ndiponso zoipa zokhazokha. Amalalira m'midzi, amapha anthu osalakwa m'malo obisalira. Amazondazonda kuti apeze opanda mwai. Amabisalira osauka ngati mkango m'ngaka yake, amabisalira osauka kuti aŵagwire. Osaukawo amaŵagwiradi akaŵakokera mu ukonde wake. Amambwandira ndi kupsitiriza anthu osoŵa mwai, ndipo nyonga zake zimaŵagwetsa pansi. Mumtima mwake amaganiza kuti, “Mulungu sasamalako, waphimba maso ake, sadzaziwona zimenezi.” Dzambatukani, Inu Chauta. Onetsani mphamvu zanu, Inu Mulungu. Musaiŵale ozunzika. Chifukwa chiyani munthu woipa amanyoza Mulungu? Chifukwa chiyani mumtima mwake amati, “Sadzandilanga?” Inutu mumaonadi, mumazindikira zovuta ndi zosautsa, kuti muchitepo kanthu. Wopanda mwai amadzipereka kwa Inu. Nayenso wamasiye mumamthandiza. Thetsani mphamvu za munthu woipa ndi wochimwa. Fufuzani kuipa kwake, ndipo mumlange kuti asadzabwerezenso. Chauta ndiye Mfumu mpaka muyaya. Mitundu ya anthu akunja idzatheratu m'dziko lake. Chauta, mumamva zimene odzichepetsa amapempha. Mudzalimbitsa mitima yao, mudzaŵatchera khutu. Potero mudzaŵateteza amasiye ndi opsinjidwa, kuti anthu amene ali a pansi pano, asadzathe kuwopsezanso. Ndimathaŵira kwa Chauta. Nanga mungathe bwanji kundiwuza kuti, “Thaŵira ku mapiri ngati mbalame. Taonani, anthu oipa akunga uta ndipo akwinja muvi pa nsinga, kuti alase anthu a mtima wolungama. Tsono ngati maziko aonongeka, nanga wolungama angachite chiyani?” Koma Chauta ali m'Nyumba yake yoyera, Chauta mpando wake waufumu uli kumwamba. Maso ake amapenya anthu onse ndi kuŵayesa. Chauta amayesa anthu olungama namakondwera nawo, mtima wake umadana ndi anthu oipa okonda zachiwawa. Iye adzaŵagwetsera makala ndi miyala yamoto ngati mvula, adzaŵalanga ndi mphepo yotentha monga kuŵayenera. Paja Chauta ndi wolungama, amakonda ntchito zolungama, ndipo anthu olungama adzaona nkhope yake. Thandizeni, Inu Chauta, palibenso munthu wosamala za Inu, okhulupirika sapezekanso pakati pa anthu. Aliyense amangonamiza mnzake, amathyasika ndi pakamwa pake, amalankhula ndi mitima iŵiri. Inu Chauta, tsekani pakamwa ponse pothyasika letsani lilime lililonse lolankhula modzikuza. Paja anthu amenewo amanena kuti, “Tidzapambana ndi mau athu, pakamwa tili napo, nanga angatigonjetse ndani?” Chifukwa choti osauka alandidwa zao ndipo osoŵa akudandaula, Chauta akunena kuti, “Ndichitapo kanthu tsopano, ndiŵapulumutsa monga momwe akufuniramo.” Malonjezo a Chauta ndi angwiro, ali ngati siliva womkometsa m'ng'anjo yamoto, woyeretsedwa kasanunkaŵiri. Titetezeni, Inu Chauta, titchinjirizeni nthaŵi zonse kwa anthu ameneŵa, pakuti anthu oipa amangoyendayenda ponseponse, ndipo anzao amayamikira zochita zao zoipa. Kodi mpaka liti, Inu Chauta? Kodi mudzandiiŵala mpaka muyaya? Kodi mudzandibisira nkhope yanu nthaŵi zonse? Kodi ndizivutika m'maganizo mwanga mpaka liti? Kodi ndiyenera kukhala ndi chisoni mumtima mwanga usana ndi usiku? Kodi mdani wanga azindipambana mpakampaka? Mundikumbukire ndipo mundiyankhe, Inu Chauta, Mulungu wanga. Mundiwunikire kuti ndingagone tulo tofa nato. Mdani wanga asati, “Ndampambana,” adani anga onse asakondwere poona kuti ndagwa. Koma ine ndimadalira chikondi chanu chosasinthika. Mtima wanga udzakondwera chifukwa mwandipulumutsa. Ndidzaimbira Chauta, popeza kuti wandichitira zabwino. Mumtima mwake munthu wopusa amati, “Kulibe Mulungu.” Anthu otereŵa ndi oipa, amachita zonyansa, palibe ndi mmodzi yemwe wochita zabwino. Chauta kumwambako waŵerama, akuyang'ana anthu pansi pano, kuti aone ngati angakhalepo mmodzi wanzeru wofunitsitsa Mulungu. Koma ai, anthu onse ndi osokera, onsewo ndi oipa chimodzimodzi. Palibe ndi mmodzi yemwe wochita zabwino, ai, palibiretu ndi mmodzi yemwe. Kani anthu oipaŵa alibe nzeru chotere? Iwo amameza anthu anga, kuŵayesa chakudya, ndipo samutama Chauta mopemba. Tsonotu iwo adzachita mantha aakulu, pakuti Mulungu amakhala pa mbali ya anthu abwino. Inu anthu oipa, mumayesa kusokoneza zolinga za anthu osauka, koma iwo amathaŵira kwa Chauta. Chibwere ndithu chipulumutso cha Israele kuchokera ku Ziyoni. Chauta akadzaŵabwezera ufulu anthu ake, Yakobe adzakondwera, Israele adzasangalala kwambiri. Inu Chauta, kodi ndani angathe kukhala m'Nyumba mwanu? Ndani angathe kukhala pa phiri lanu loyera? Ndi munthu amene amayenda mosalakwa, amene amachita zolungama nthaŵi zonse, amene amalankhula zinthu ndi mtima woona. Ndi amene sasinjirira ndipo sachita anzake zoipa, kapena kumafalitsa mbiri yoipa ya anzake. Ndi amene amanyoza munthu womkana Mulungu, koma amalemekeza anthu omvera Chauta. Ndi amene amachitadi zimene walonjeza, ngakhale zikhale zoŵaŵa chotani. Ndi amene sakongoza ndalama zake kuti alandire chiwongoladzanja, amene salandira chiphuphu kuti azunze munthu wosalakwa. Munthu wochita zimenezi, palibe chilichonse chimene chidzamgwedeze. Mundisunge Inu Mulungu, pakuti ndikuthaŵira kwa Inu. Ndimamuuza Chauta kuti, “Inu ndinu Ambuye anga. Ndilibe chinthu china chabwino koma Inu nokha.” Kunena za oyera mtima amene ali pansi pano, ameneŵa ndi olemekezeka, ndipo ndimakondwera nawo. Amene amasankhula milungu ina, amadzichulukitsira mavuto. Sindidzatsira nawo nsembe zao zamagazi kapena kutchula maina a milungu yaoyo. Chauta ndiye chuma changa ndi choloŵa changa. Tsogolo langa lili m'manja mwanu. Malire a malo anga andikhalira mwabwino. Inde, ndalandira madalitso abwino ndithu. Ndikutamanda Chauta amene ali phungu wanga. Mtima wanga umandilangiza ndi usiku womwe. Nthaŵi zonse ndimalingalira za Chauta. Popeza kuti ali ku dzanja langa lamanja, palibe amene angandiopse konse. Nchifukwa chake mtima wanga ukukondwa, ndipo m'katikati mwangamu ndikusangalala. Thupi langanso lidzakhala pabwino, chifukwa simudzandisiya ku malo a anthu akufa, simudzalola kuti wokondedwa wanune ndikaole kumeneko. Mumandiwonetsa njira ya ku moyo. Ndimapeza chimwemwe chachikulu kumene kuli Inu, ndidzasangalala mpaka muyaya ku dzanja lanu lamanja. Inu Chauta, imvani pemphero la ine munthu wolungama, imvani kupemba kwanga. Tcherani khutu kuti mumve mau ochokera kwa ine, munthu wosanyengane. Kusalakwa kwanga kuwonekere poyera pa chiweruzo chanu, maso anu aone kulungama kwanga. Ngakhale muyese mtima wanga, kapena kundipenyetsetsa usiku, kaya mundiyang'anitsitse chotani, mudzapeza kuti ndilibe mlandu. Pakamwa panga sipalankhula zoipa. Kunena za ntchito za anthu, ine posunga mau anu, sindidatsate za anthu andeu. Ndayenda m'njira zanu nthaŵi zonse, sindidapatuke konse. Ndikupemphera kwa Inu Mulungu, chifukwa mudzandiyankha. Tcherani khutu kuti mumve mau anga. Onetsani chifundo chanu pakuchita zodabwitsa, Inu amene mumaŵapulumutsa ndi dzanja lanu lamanja onse obwera kwa Inu, kuthaŵa adani ao. Mundisunge ngati mwana wa diso, munditeteze pansi pa mapiko anu, kuti asandiwone anthu oipa ofuna kupasula, ndiye kuti adani anga oopsaŵa amene akundizinga. Mitima yao ilibe chifundo, amalankhula modzikuza. Amangondilondola ndi kundizinga. Amandiyang'ana kuti apeze njira yondigwetsera pansi. Ali ngati mkango wofunitsitsa kuti ukadzule, ngati chilombo cholusa cholalira. Dzambatukani, Inu Chauta, mukumane nawo ndi kuŵagonjetsa. Mundipulumutse ndi lupanga lanu kwa anthu oipawo. Inu Chauta, ndi dzanja lanu mundilanditse kwa adani, kwa anthu amene moyo wao umangosamala zapansipano. Muŵalange ndi zoŵaŵa zimene mudaŵasungira. Nawonso ana awo akhale nazo zambiri, ndipo iwowo asiyireko ana aonso. Koma ine m'kulungama kwanga ndidzaona nkhope yanu. Tsono ine nditadzuka, ndidzakondwa kotheratu poonana ndi Inu. Ndimakukondani Chauta, Inu mphamvu zanga. Chauta ndiye thanthwe langa, linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndiye Mulungu wanga, ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga, ndiye linga langa. Ndimaitana Chauta, amene ayenera kumtamanda, ndipo amandipulumutsa kwa adani anga. Nthambo za imfa zidandizungulira, mitsinje yothamanga yoononga idandisefukira. Nthambo zakumanda zidandizeŵeza, misampha ya imfa idandikola. Ndidaitana Chauta m'zovuta zanga. Ndidafuulira Mulungu wanga kuti andithandize. Iye ali m'Nyumba mwake, adamva liwu langa, kulira kwanga kofuna chithandizo kudamveka kwa iye. Pamenepo dziko lapansi lidanjenjemera ndi kuchita chivomezi. Maziko a mapiri nawonso adanjenjemera ndi kugwedezeka, chifukwa Iye adaakalipa. M'mphuno mwake munkafuka utsi, m'kamwa mwake munkatuluka moto woononga, makala amoto anali laŵilaŵi kuchokera m'kamwa momwemo. Adang'amba thambo natsika pansi, mdima wabii unali ku mapazi ake. Adakwera pa mkerubi nauluka. Adayenda mwaliŵiro ndi mphepo. Mdima adausandutsa chofunda chake, mitambo yakuda yamvula adaisandutsa mwafuli wake. M'kuŵala kumene kunali pamaso pake, munkafumira matalala ndi makala amoto, amene adabzola mitambo yophimba ija. Kumwamba Chauta adagunda ngati bingu, Wopambanazonse liwu lake lidamveka m'kati mwa matalala ndi makala amoto. Adaponya mivi yake nabalalitsa adani ake, adachititsa zing'aning'ani, naŵapirikitsa. Ngalande zozama zam'nyanja zidaonekera, maziko a dziko lapansi adakhala poyera, pamene Inu Chauta mudakhuluma mokalipa, pamene mudatulutsa mpweya wamphamvu m'mphuno mwanu. Ali kumwamba Chauta adatambalitsa dzanja nandigwira, ndi kundivuula m'madzi ozama. Adandipulumutsa kwa adani anga amphamvu, kwa onse amene ankadana nane, pakuti iwo anali amphamvu kwambiri kupambana ine. Adaniwo adandithira nkhondo pamene ndinali m'mavuto, koma Chauta adandichirikiza. Adakandifikitsa ku malo amtendere, adandipulumutsa chifukwa adakondwera nane. Chauta adandipatsa mphotho molingana ndi ntchito zanga zabwino, adandifupa molingana ndi ungwiro wanga. Ine ndidatsata njira za Chauta, sindidachite zoipa ndi kumsiya Mulungu wanga. Ndidamvera malangizo ake onse, ndipo malamulo ake sindidaŵataye. Ndinalibe mlandu pamaso pake, ndinkalewa zoipa m'moyo mwanga. Nchifukwa chake Chauta wandipatsa mphotho molingana ndi ntchito zanga zabwino, monga momwe akuwonera kuti ndilibe mlandu. Kwa anthu okhulupirika, Inu Mulungu mumadziwonetsa okhulupirika. Kwa anthu aungwiro, mumadziwonetsa abwino kotheratu. Kwa anthu oyera mtima mumadziwonetsa okoma mtima, koma kwa anthu oipa mtima, mumawonetsa kunyansidwa nawo. Paja anthu odzichepetsa, Inu mumaŵapulumutsa, koma anthu odzikuza mumaŵatsitsa. Ndithu, Inu mumayatsa nyale ya moyo wanga. Chauta, Mulungu wanga, amandiwunikira mu mdima. Ndi chithandizo chanu ndingathe kugonjetsa gulu la ankhondo. Ndi chithangato cha Mulungu, ndingathe kupambana. Mulungu wathuyo, zochita zake nzangwiro, mau ake sapita pachabe, Iye ndiye chishango choteteza onse othaŵira kwa Iye. Palibe mulungu wina koma Chauta yekha. Palibe thanthwe lina lothaŵirapo koma Mulungu wathu yekha. Mulungu wathu ndiye amene amandiveka mphamvu, wandichotsera zoopsa m'njira zanga. Amalimbitsa miyendo yanga ngati ya mbaŵala, ndipo amandisunga bwino m'mapiri. Amaphunzitsa manja anga kamenyedwe ka nkhondo, kotero kuti ndingathe kupinda uta wachitsulo. Inu mwanditchinjiriza ndi chishango chanu chachipulumutso. Dzanja lanu lamanja landichirikiza, mwandikweza ndi chithandizo chanu. Mudandikuzira njira yanga kuti ndiyendemo bwino, choncho mapazi anga sadaterereke. Ndidalondola adani anga ndi kuŵapeza, sindidabwerere mpaka nditaŵagonjetsa. Ndimaŵakantha koopsa kotero kuti sangathenso kudzuka, ndidaŵapondereza ndi mapazi anga. Paja ndinu mudandipatsa mphamvu zomenyera nkhondo, ndinu mudandigonjetsera anthu ondiwukira. Inu mudapirikitsa adani anga kuti andithaŵe, amene ankadana nane ndidaŵaononga. Adakuwa kuti ena aŵathandize, koma panalibe woŵapulumutsa. Adalirira Chauta, koma sadaŵayankhe. Ndidaŵaperapera ngati fumbi louluka ndi mphepo. Ndimaŵapondereza ngati matope amumseu. Inu mudandipulumutsa kwa anthu olimbana nane, Inu mudandisandutsa mfumu ya mitundu yonse. Choncho anthu osaŵadziŵa ankanditumikira. Atangomva za ine adayamba kundimvera, anthu a maiko ena adabwera kwa ine kudzapemba. Anthu a mitundu ina adataya mtima, adatuluka m'malinga mwao ali njenjenje. Chauta ndi wamoyo. Litamandike thanthwe langa, alemekezeke Mulungu wondipulumutsa, Mulungu ndiye adandithandiza kuti ndilipsire, adagonjetsa anthu a mitundu ina, kuti akhale mu ulamuliro wanga. Ndiye amene adandipulumutsa kwa adani anga. Zoonadi Inu mudandikweza pamwamba pa ondiwukira, mudandilanditsa kwa anthu ankhanza. Chifukwa cha zimenezi ndidzakutamandani Inu Chauta, pakati pa mitundu ya anthu, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu. Mulungu amathandiza mfumu yake, kuti izipambana nthaŵi ndi nthaŵi. Amaonetsa chikondi chake chosasinthika kwa wodzozedwa wake, ndiye kuti kwa Davide ndi kwa zidzukulu zake mpaka muyaya. Zakumwamba zimalalika ulemerero wa Mulungu, thambo limasonyeza ntchito za manja ake. Usana umasimbira zimenezo usana unzake, usiku umadziŵitsa zimenezo usiku unzake. Palibe kulankhula, palibe kunena mau aliwonse. Liwu lao silimveka konse. Komabe uthenga wao umafalikira pa dziko lonse lapansi. Mau aowo amafika mpaka ku mathero a dziko. Mulungu adamangira dzuŵa nyumba m'thambomo. Dzuŵalo limatuluka ngati mkwati wokondwa amene akutuluka m'nyumba mwake, ndipo limayenda ndi chimwemwe ngati ngwazi yamphamvu. Limatuluka kuyambira ku mathero ena a thambo, ndi kuzungulira mpaka ku mathero enanso. Palibe chinthu chilichonse chotha kulewa kutentha kwake. Mau a Chauta ngangwiro, amapatsa munthu moyo watsopano. Umboni wa Chauta ndi wokhulupirika, umaŵapatsa nzeru amene alibe. Malangizo a Chauta ndi olungama, amasangalatsa mtima. Malamulo a Chauta ndi olungama, amapatsa mtima womvetsa. Kuwopa Chauta ndiye chinthu changwiro, chimakhala mpaka muyaya. Chiweruzo cha Chauta nchoona, ncholungama nthaŵi zonse. Zonsezi nzoyenera kuzikhumbira kupambana golide, ngakhale golide wambiri wamtengowapatali, nzotsekemera kupambana uchi, ngakhale uchi wozuna kwambiri. Malamulo anu amandiwunikira ine mtumiki wanu, poŵasunga ndimalandira mphotho yaikulu. Nanga ndani angathe kudziŵa zolakwa zake? Inu Chauta, mundichotsere zolakwa zanga zobisika. Musalole kuti ine mtumiki wanu ndizichimwa dala, kulakwa koteroku ndisakutsate. Tsono ndidzakhala wangwiro wopanda mlandu wa uchimo waukulu. Mau anga ndi maganizo anga avomerezeke pamaso panu, Inu Chauta, thanthwe langa ndi mpulumutsi wanga. Chauta akuthandize pa tsiku lamavuto. Mulungu wa Yakobe akuteteze. Akutumizire chithandizo kuchokera ku malo ake oyera, akuchirikize kuchokera ku Ziyoni. Alandire zopereka zako zonse, akondwere ndi nsembe zako zopsereza. Akupatse zimene mtima wako ukukhumba, akuthandize kuti zonse zimene wakonza zichitikedi. Choncho tifuule ndi chimwemwe chifukwa chakuti mwapambana pa nkhondo, tikweze mbendera kutamanda dzina la Mulungu wathu. Chauta akupatse zonse zimene wapempha. Tsopano ndikudziŵa kuti Chauta adzathandiza wodzozedwa wake. Adzamuyankha ali ku malo ake oyera kumwamba, pakumpambanitsa kwathunthu ndi dzanja lake lamanja. Ena amatamira magaleta ankhondo, ena amadalira akavalo, koma ife timatamira dzina la Chauta, Mulungu wathu, timamutama Iyeyo mopemba. Adani adzaphofomoka ndi kugwa, koma ife tidzadzuka kukhala chilili. Inu Chauta, thandizani mfumu kuti ipambane. Mutiyankhe pamene tikuitana. Mfumu ikusangalala chifukwa mwaipatsa mphamvu, Inu Chauta, ikukondwa kwambiri chifukwa mwaipambanitsa ndinu. Mwaipatsa zimene mtima wake umakhumba, simudaimane zimene pakamwa pake padapempha. Mumafika kwa mfumuyo ndi madalitso okoma kwambiri. Mwaiveka chipewa chaufumu chagolide pamutu. Iyo idakupemphani moyo, ndipo Inu mudaipatsa moyo wautali, wamuyaya. Ulemerero wake ndi waukulu chifukwa mwaipambanitsa ndinu. Mwaipatsa ufumu waukulu ndi waulemu. Zoonadi, mwaisandutsa yodala kopambana mpaka muyaya. Mwaisangalatsa ndi chimwemwe, chifukwa muli nayo. Paja mfumuyo imakhulupirira Chauta, ndipo siidzagwedezeka chifukwa cha chikondi chosasinthika cha Wopambanazonse. Idzagonjetsa adani ake onse. Dzanja lake lamphamvu lidzakantha onse odana nayo. Ikangotulukira, idzaŵaononga monga m'mene ng'anjo yamoto imaonongera. Chauta adzaŵatha phu, chifukwa cha kukwiya nawo, ndipo iwo adzanyeka ndi moto kuchita kuti psiti. Mfumuyo idzaononga ana ao pa dziko lapansi, zidzukulu zao zidzatha pakati pa anthu. Akafuna kuti aichite choipa ndi kuipweteka, adzalephereratu, pakuti idzaŵapirikitsa potendekera nkhope zao ndi mauta ake. Mutamandike, Inu Chauta, chifukwa cha kupambana kwanu. Tidzaimba ndi kuyamika mphamvu zanu zazikulu. Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji? Chifukwa chiyani simukundithandiza mpang'ono pomwe, chifukwa chiyani simukumva mau a kubuula kwanga? Mulungu wanga, ine ndimalira usana, koma Inu simundiyankha, ndimalira usiku, koma sindipeza mpumulo. Komabe Inu ndinu oyera, mumakhala pa mpando wanu waufumu, ndipo anthu anu Aisraele amakutamandani. Makolo athu ankadalira Inu. Zoonadi, ankakhulupirira Inu, ndipo Inu munkaŵapulumutsa. Ankalirira Inu, ndipo Inu munkaŵalanditsa. Ankakhulupirira Inu, ndipo Inu simunkaŵagwiritsa mwala. Koma ine ndine nyongolotsi, sindine munthu konse, ndine amene anthu onse amandinyodola ndi kundinyoza. Onse ondiwona amandiseka, amandikwenzulira ndi kupukusa mitu yao. Amati, “Unkadalira Chauta, Chauta yemweyo akupulumutse. Akulanditsetu tsono, popeza kuti amakukonda.” Komabe Inu ndinu amene mudalola kuti ndibadwe. Inu ndinu chikhulupiriro changa, mudandilera bwino ndili mwana woyamwa. Ndakhala ndikudalira Inu chibadwire changa, Inu mwakhala Mulungu wanga kuyambira pamene mai wanga adandibala. Musandikhalire kutali, pakuti mavuto ali pafupi kundigwera, ndipo palibe wina wondithandiza. Nkhunzi zambiri zandizungulira. Adani amphamvu ngati nkhunzi za ku Basani andizinga. Andiyasamira kukamwa, ngati mkango wobangula wofuna kundikadzula. Moyo wanga watayika ngati madzi, mafupa anga aweyeseka. Mtima wanga uli ngati sera, wasungunuka m'kati mwanga. Kukhosi kwanga kwauma ngati phale, lilime langa lakangamira ku nsagwada. Inu mwandisiya pa fumbi kuti ndifere pomwepo. Anthu ankhanza andizinga ngati mimbulu. Aboola manja anga ndi mapazi anga. Mafupa anga akuwonekera, koma anthu aja akungondiyang'anitsitsa akukondwera poona kuti ndikuvutika. Agaŵana zovala zanga, ndipo achitira malaya anga maere. Koma Inu Chauta musakhale kutali. Inu, mphamvu zanga, fulumirani kudzandithandiza. Pulumutsani moyo wanga ku lupanga. Landitseni ku mphamvu za mimbulu. Pulumutseni kukamwa kwa mkango, mulanditse moyo wanga wovutika ku nyanga za njati. Ndidzasimbira abale anga za dzina lanu. Ndidzatamanda dzina lanu pa msonkhano wa anthu anu. Ndidzati, “Inu omvera Chauta, mtamandeni Iye. Inu nonse ana a Yakobe mlemekezeni Iye, inu nonse ana a Israele, mchitireni Iye ulemu. “Pakuti sadanyoze munthu wozunzika, sadaipidwe ndi masautso ake, sadamubisire nkhope yake, koma adamumvera pamene adamdandaulira.” Ndidzakutamandani pa msonkhano waukulu chifukwa cha zimene mwandichitira. Zimene ndidalonjeza ndidzazichita pamaso pa onse okumverani. Ozunzika adzadya ndi kukhuta, ofunafuna Chauta adzamtamanda. Ine ndidzati, “Mitima yanu ikhale ndi moyo nthaŵi zonse.” Anthu a mitundu yonse pa dziko lapansi adzakumbukira nadzatembenukira kwa Chauta, mabanja a mitundu ina ya anthu adzampembedza. Pakuti ulamuliro ndi wake wa Chauta, Iye amalamula anthu a mitundu yonse. Anthu onse odzitama adzamuŵeramira. Anthu onse oloŵa m'manda nawonso adzamugwadira, ndiye kuti onse osatha kudzisungira moyo. Zidzukulu zam'tsogolo zidzatumikira Ambuye. Anthu adzauza mbadwo umene ukudzawo za Iye. Adzalalika za chipulumutso chake kwa anthu amene mpaka tsopano sanabadwe, ponena kuti Chauta ndiye adapulumutsa anthu ake. Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasoŵa kanthu. Amandigoneka pa busa lamsipu. Amanditsogolera ku madzi odikha kokapumulirako. Amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera m'njira za chilungamo malinga ndi ulemerero wa dzina lake. Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza. Inu mumandikonzera chakudya, adani anga akuwona. Mumandilandira bwino podzoza mutu wanga ndi mafuta, mumadzaza chikho changa mpaka kusefukira. Zoonadi, zokoma zanu ndi chikondi chanu zidzakhala ndi ine masiku onse a moyo wanga. Ndidzakhala m'Nyumba mwanu moyo wanga wonse. Dziko lapansi ndi zonse zam'menemo ndi za Chauta, dziko lonse lapansi pamodzi ndi anthu onse okhalamo ndi ake. Pakuti iye ndi amene adaika dziko lapansi pa nyanja yaikulu, adalikhazika pa mitsinje yozama. Ndani angayenere kukwera phiri la Chauta? Ndani angaime m'malo ake oyera? Ndi amene amachita zabwino ndi manja ake, ndipo amaganiza zabwino mumtima mwake. Ndi amene salingalira zonama, ndipo salumbira monyenga. Adzalandira madalitso kwa Chauta, ndipo Mulungu Mpulumutsi wake adzagamula kuti alibe mlandu. Anthu otere ndiwo amene amafunitsitsa Chauta, ndiwo amene amabwera kudzapembedza Mulungu wa Yakobe. Kankhani zipata za mzinda, tsekulani zitseko zakalekalezo, kuti Mfumu yaulemerero iloŵe. Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani? Ndi Chauta wanyonga ndi wamphamvu, Chauta ndiye ngwazi pa nkhondo. Kankhani zipata za mzinda, tsekulani zitseko zakalekalezo, kuti Mfumu yaulemerero iloŵe. Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani? Ndi Chauta Wamphamvuzonse. Iyeyo ndiye Mfumu yaulemerero. Ndikupereka mtima wanga kwa Inu Chauta. Ndikuika mtima wanga pa Inu Mulungu wanga. Musalole kuti adani anga andichititse manyazi, musalole kuti akondwere pamene ine ndikuvutika. Zoonadi, onse okhulupirira Inu asaŵachititse manyazi, koma muchititse manyazi onse ochita dala zosakhulupirika. Mundidziŵitse njira zanu, Inu Chauta, mundiphunzitse kuchita kufuna kwanu. Munditsogolere m'choona chanu ndi kundilangiza, pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga, ndimadalira Inu masiku onse. Inu Chauta, kumbukirani chifundo chanu ndi chikondi chanu chosasinthika, chifukwa mudaziwonetsa kuyambira kalekale. Musakumbukire machimo a unyamata wanga ndi mphulupulu zanga. Koma mundikomere mtima, Inu Chauta, chifukwa cha chikondi chanu, pakuti Inu ndinu abwino. Chauta ndi wabwino ndi wolungama. Nchifukwa chake amaphunzitsa ochimwa njira zake. Amatsogolera anthu odzichepetsa kuti achite zolungama, amaŵaphunzitsa njira zake. Njira zonse za Chauta ndi za chikondi chosasinthika, nzokhulupirika kwa anthu osunga chipangano chake ndi malamulo ake. Malinga ndi ulemerero wa dzina lanu, Inu Chauta, mundikhululukire machimo anga pakuti mlandu wanga ndi waukulu. Kodi pali munthu woopa Chauta? Munthuyo Chauta adzamphunzitsa njira yoti aitsate. Munthu ameneyo adzakhaladi pabwino, ana ake adzalandira dziko kuti likhale choloŵa chao. Chauta amapalana chibwenzi ndi anthu omvera Iye, ndipo amaŵadziŵitsa chipangano chake. Maso anga akuyang'ana kwa Chauta nthaŵi zonse, pakuti adzaonjola mapazi anga mu ukonde. Inu Chauta yang'aneni ine, ndipo mundikomere mtima, pakuti ndili ndekhandekha, ndipo ndazunzika kwambiri. Mundichotsere nkhaŵa za mumtima mwanga, ndipo munditulutse m'masautso anga. Penyani mazunzo anga ndi mavuto anga, ndipo mundikhululukire machimo anga onse. Onani m'mene adani anga ankhalwe achulukira ndi m'mene chidani chao ndi ine chakulira. Tchinjirizani moyo wanga ndi kundipulumutsa. Musalole kuti andichititse manyazi, pakuti ndikuthaŵira kwa Inu. Kukhulupirika kwanga ndi kulungama kwanga kunditeteze, popeza kuti ndakukhulupirirani. Inu Mulungu apulumutseni m'mavuto ao onse anthu anu Aisraele. Inu Chauta, onetsani kuti ine ndine wosalakwa, pakuti ndimachita zolungama, ndipo ndakhulupirira Inu mosakayika konse. Mundiyang'anitsitse, Inu Chauta, ndi kundiyesa. Muwone mtima wanga pamodzi ndi maganizo anga. Chikondi chanu chimanditsogolera, ndipo ndimakhala wokhulupirika kwa Inu. Sindikhala pamodzi ndi anthu onyenga, sindiyenda ndi anthu achiphamaso. Ndimadana ndi anthu ochita zoipa, sindikhala pamodzi ndi anthu oipa. Ndimasamba m'manja kuwonetsa kuti sindidachimwe, ndimakupembedzani pa guwa lanu lansembe, Inu Chauta. Ndimaimba molimbika nyimbo yothokozera, ndimalalika ntchito zanu zonse zodabwitsa. Inu Chauta, ndimakonda Nyumba imene mumakhalamo, ndiye kuti malo amene kuli ulemerero wanu. Musanditayire kumodzi ndi anthu ochimwa, musandichotsere moyo pamodzi ndi anthu ofuna kupha anzao, anthu amene manja ao amachita zoipa, ndipo anthu amene dzanja lao lamanja ndi lodzaza ndi ziphuphu. Koma ine ndimayenda mokhulupirika, mundikomere mtima ndipo mundipulumutse. Ndili wokhazikika pa malo opanda zovuta, ndipo ndidzatamanda Chauta pa msonkhano waukulu. Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha? Pamene adani ndi amaliwongo anga andiputa kuti andiphe, adzaphunthwa ndipo adzagwa. Ngakhale gulu lankhondo lindizinge, mtima wanga sudzachita mantha konse. Ngakhale nkhondo ibuke kulimbana nane, ine sindidzaleka kukhulupirira. Ndapempha chinthu chimodzi chokha kwa Chauta, chinthu chofunika kwambiri, chakuti ndizikhala m'Nyumba ya Chauta masiku onse a moyo wanga, kuti ndizikondwera ndi kukoma kwake kwa Chauta ndi kuti ndizipembedza Iye m'Nyumba mwakemo. Pa tsiku lamavuto adzandibisa ndi kunditchinjiriza. Adzandisunga m'kati mwa Nyumba yake, adzanditeteza pa thanthwe lalitali. Ndidzapambana adani anga ondizungulira, ndipo ndidzapereka nsembe m'Nyumba mwake ndili kufuula ndi chimwemwe. Ndidzaimba nyimbo yotamanda Chauta. Imvani, Inu Chauta, pamene ndikulira mofuula, mundikomere mtima ndi kundiyankha. Pajatu Inu mudati, “Muzifunafuna nkhope yanga.” Inu Chauta, ndidzafunafuna nkhope yanu. Musandibisire nkhope yanu. Musandipirikitse ine mtumiki wanu mokwiya, Inu amene mwakhala mukundithandiza. Musanditaye, musandisiye ndekha, Inu Mulungu Mpulumutsi wanga. Ngakhale bambo wanga ndi mai wanga andisiye ndekha, Inu Chauta mudzandisamala. Mundiwonetse njira zanu zachifundo, Inu Chauta, munditsogolere m'njira yosalala, chifukwa ndili ndi adani ambiri. Musandipereke m'manja mwa adani angawo. Mboni zonama zandiwukira, ndipo zimandiwopseza. Ndikhulupirira kuti ndidzaona ubwino wake wa Chauta m'dziko la amoyo. Tsono khulupirira Chauta. Khala wamphamvu, ndipo ulimbe mtima. Ndithu, khulupirira Chauta. Ndikuitana Inu Chauta, Inu thanthwe langa, musachite ngati simukundimva, chifukwa ngati mukhala chete, ndidzafanafana ndi anthu otsikira ku manda. Imvani kupempha kwanga, pamene ndikulirira Inu kuti mundithandize, pamene ndikukupembedzani pokweza manja anga ku malo anu opatulika kopambana. Musandichotsere kumodzi ndi anthu oipa, anthu amene amachita zonyenga, amene amalankhula zamtendere ndi anzao, koma mitima yao ndi yodzaza ndi chidani. Muŵabwezere anthu otere molingana ndi ntchito zao, muŵalange molingana ndi zoipa zimene ankachita. Muŵabwezere molingana ndi ntchito zao, Muŵalange molingana ndi kuipa kwa ntchito zao. Chifukwa chakuti iwo sasamalako ntchito za Chauta, ngakhale zimene adalenga Iye. Chauta adzaŵagumula ngati nyumba, osaŵamanganso. Chauta atamandike, pakuti wamva liwu la kupempha kwanga. Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiyenso chishango changa chonditeteza. Ndaika mtima wanga wonse pa Iye. Wandithandiza, choncho mtima wanga ukusangalala, ndipo ndimamthokoza ndi nyimbo yanga. Chauta ndiye mphamvu zimene anthu ake amadalira, ndiye kothaŵira komwe wodzozedwa wake amapulumukirako. Pulumutsani anthu anu, Inu Chauta, mudalitse amene mudaŵasankha. Mukhale mbusa wao, muŵasamale mpaka muyaya. Tamandani Chauta, inu okhala kumwamba. Tamandani ulemerero wake ndi mphamvu zake. Tamandani ulemerero wa dzina la Chauta. Mumpembedze mu ulemu wa ungwiro wake. Liwu la Chauta likumveka pamwamba pa nyanja. Mulungu waulemerero wachita bingu, liwu lake lamveka pa nyanja yaikulu. Liwu la Chauta ndi lamphamvu, liwu la Chauta ndi laulamuliro. Liwu la Chauta limathyola mikungudza, Chauta amathyolathyoladi mikungudza ya ku Lebanoni. Amagwedeza phiri la Lebanoni kuti lizivinavina ngati likonyani, amavinitsa phiri la Sirioni ngati mwanawanjati. Liwu la Chauta likutulutsa malaŵi amoto. Liwu la Chauta likugwedeza chipululu, Chauta akugwedeza chipululu cha Kadesi. Liwu la Chauta likuzunguza miŵanga likupulula masamba a mitengo yonse m'dondo. Onse a m'nyumba mwake akufuula kuti, “Ulemererowo!” Chauta amalamulira nyanja zonse, amakhala kwamuyaya pa mpando wake wachifumu. Chauta amapatsa anthu ake mphamvu. Amaŵadalitsa anthu ndi mtendere. Salmo la Davide. Nyimbo yoimba potsekula Nyumba ya Mulungu Ndidzakutamandani, Inu Chauta, pakuti mwanditulutsa m'dzenje la imfa. Simudalole kuti adani anga akondwere poona kuti ndikuvutika. Chauta, Mulungu wanga, ndidalirira Inu kuti mundithandize, ndipo mwandichiritsa. Inu Chauta, mwanditulutsa m'dziko la akufa, mwandibwezeranso moyo kuti ndingatsikire ku manda. Imbani nyimbo zotamanda Chauta, inu anthu ake oyera mtima, mumthokoze chifukwa cha dzina lake loyera. Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha. Koma ine, pamene zinthu zidaandiyendera bwino, ndidati, “Sindidzagwedezeka konse.” Chifukwa cha kukoma mtima kwanu, Inu Chauta, mudandikhazikitsa ngati phiri lolimba. Koma pamene mudandimana madalitso anu, ine ndidataya mtima. Pamenepo ndidalirira Inu Chauta, ndipo ndidapempha chifundo chanu kuti, “Kodi mudzapindulanji pa imfa yanga ngati nditsikira ku manda? Kodi ine nditasanduka fumbi, ndingathe kukutamandani? Kodi pamenepo ndingathe kulalika za kukhulupirika kwanu? “Imvani, Inu Chauta, ndipo mundikomere mtima. Inu Chauta, mukhale mthandizi wanga.” Mwasandutsa kulira kwanga kuti kukhale kuvina, mwachotsa chisoni changa ndi kundipatsa chisangalalo. Choncho ndisakhale chete, koma ndikutamandeni ndi mtima wonse. Choncho mtima wanga udzakuimbirani mosalekeza, Chauta, Mulungu wanga, ndidzakuthokozani mpaka muyaya. Ndimathaŵira kwa Inu Chauta, musalole kuti ndichite manyazi, koma mundipulumutse chifukwa ndinu Mulungu wolungama. Tcherani khutu kuti mundimve, fulumirani kudzandipulumutsa. Mukhale thanthwe langa lothaŵirako, ndi linga langa lolimba londipulumutsa. Zoonadi, ndinu thanthwe langa ndi linga langa. Tsogolereni ndi kundiwongolera chifukwa Inu ndinu Chauta. Onjoleni mu ukonde umene anditchera, pakuti Inu ndinu pothaŵira panga. Ndikupereka moyo wanga m'manja mwanu. Inu Chauta wokhulupirika, mwandiwombola. Inu mumadana ndi opembedza mafano achabechabe. Koma ine ndimakhulupirira Inu Chauta. Ndidzakondwa ndi kusangalala chifukwa ndinu a chikondi chosasinthika. Mwaona masautso anga, mwazindikira mavuto anga kuti ndi aakulu. Simudandipereke m'manja mwa adani anga, koma mwandiika pa malo otambalala. Tsono mundikomere mtima, Inu Chauta, pakuti ndili m'zovuta. Maso anga atupa chifukwa cha chisoni. Mumtima mwanga ndi m'thupi momwe mwadzaza zovuta. Moyo wanga ukutha chifukwa cha chisoni, zaka zanganso zikutha chifukwa cha kulira kwambiri. Mphamvu zanga zatheratu chifukwa cha kulakwa kwanga, mafupa anga agooka. Adani anga onse amandinyodola, anzanga omwe amandiyesa chinthu chonyansa. Anthu odziŵana nawo amandiyesa chinthu choopsa. Anthu ondiwona mu mseu amandithaŵa. Andiiŵala kotheratu ngati munthu wakufa. Ndasanduka ngati chiŵiya chosweka. Zoonadi, ndimamva anthu ambiri akunong'onezana zoipa za ine, zoopsa zandizinga ponseponse. Amapangana zoti andiwukire, namachita upo woipa woti andiphe. Koma ndimadalira Inu Chauta, ndimati, “Inu ndinu Mulungu wanga.” Masiku anga ali m'manja mwanu. Pulumutseni kwa adani anga ndi kwa ondizunza. Yang'aneni mtumiki wanune mwa kukoma mtima kwanu, pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika. Inu Chauta, musalole kuti ndichite manyazi, chifukwa ndapemphera kwa Inu. Koma anthu oipa ndiwo achite manyazi, apite ku manda kachetechete. Onse onyada ndi onama olankhula mwamwano ndi monyoza kwa anthu abwino, muŵakhalitse chete. Ndi waukulu ubwino wanu umene mwaŵasungira anthu okumverani, umene mwaŵachitira anthu othaŵira kwa Inu, aliyense waona zimenezi. Mumaŵabisa pamalo pamene pali Inu, kuti muŵateteze ku ziwembu za adani ao. Mumaŵasunga bwino ndi kuŵatchinjiriza, kuti anthu angakangane nawo. Atamandike Chauta: wandiwonetsa modabwitsa chikondi chake chosasinthika, pamene ndinali mu mzinda wozingidwa ndi gulu la ankhondo. Ndidalankhula mwankhaŵa kuti, “Andipirikitsira kutali ndi Inu.” Koma Inu mudamva kupempha kwanga pamene ndidakudandaulirani kuti mundithandize. Kondani Chauta, inu nonse anthu oyera mtima. Chauta amasunga anthu okhulupirika, koma amalanga koopsa anthu odzikuza. Khalani amphamvu ndipo mulimbe mtima, inu nonse okhulupirira Chauta. Ngwodala amene zolakwa zake zakhululukidwa, amene machimo ake afafanizidwa. Ngwodala amene Chauta samuŵerengera mlandu wake, amene mumtima mwake mulibe zonyenga. Pamene ndinali ndisanaulule tchimo langa, thupi langa linali lofooka, chifukwa cha kubuula tsiku lonse. Pakuti usana ndi usiku dzanja lanu lidandipsinja, motero nyonga zanga zidatha, monga amafotera masamba ndi dzuŵa lachilimwe. Koma ndidavomera tchimo langa kwa Inu, sindidabise kuipa kwanga. Ndidati, “Ndidzaulula machimo anga kwa Chauta,” pomwepo Inu mudakhululukiradi mlandu wa machimo anga. Nchifukwa chake munthu aliyense wosamala za Inu apemphere kwa Inu. Akadzafika mavuto, akadzafika madzi a chigumula, zonsezo sizidzamufika. Inu ndinu kobisalira kwanga. Inu mumanditchinjiriza nthaŵi yamavuto. Nchifukwa chake ndimaimba nyimbo zotamanda chipulumutso chanu. Chauta akuti, “Ndidzakudziŵitsa ndi kukuphunzitsa njira imene uyenera kuyendamo. Ndidzakulangiza ndi kukuyang'anira. “Musakhale opanda nzeru ngati kavalo kapena bulu amene ayenera kumuwongolera ndi chitsulo cham'kamwa ndi chapamutu, chifukwa ukapanda kutero, nyamazo sizidzakumvera.” Anthu oipa amapeza zoŵaŵa zambiri, koma munthu wokhulupirira Chauta amazingidwa ndi chikondi chosasinthika. Sangalalani ndi kukondwa inu nonse okonda Mulungu, chifukwa cha zimene Chautayo adakuchitirani. Inu anthu ake onse, fuulani ndi chimwemwe. Kondwerani mwa Chauta, inu anthu ake. Zoonadi ochita zolungama azitamanda. Tamandani Chauta ndi pangwe. Muimbireni nyimbo ndi zeze wa nsambo khumi. Muimbireni nyimbo yatsopano, kodolani nsambozo mwaluso ndi kufuula mosangalala. Mau a Chauta ndi olungama, zochita zake zonse amazichita mokhulupirika. Iye amachita zolungama ndi kuweruza mosakondera. Amaonetsa chikondi chosasinthika pa dziko lonse lapansi. Chauta adalankhula ndipo zakumwamba zidalengedwa. Zonse zakumeneko zidalengedwa pamene Iye adalankhula mau ake. Adasonkhanitsa pamodzi madzi a m'nyanja zakuya ndipo adaziikira malire kuti zisasefukire. Dziko lonse lapansi liwope Chauta. Anthu onse okhala pa dziko lapansi achite naye mantha, pakuti Iye adalankhula, ndipo zidachitikadi, adalamula, ndipo zidaonekadi. Zolinga za anthu akunja Chauta amazisandutsa zopandapake. Maganizo ao onse amaŵasandutsa achabechabe. Koma zolinga za Chauta zimachitika nthaŵi zonse, maganizo a mumtima mwake amakhazikika mpaka muyaya. Ngwodala mtundu wa anthu amene Mulungu wao ndi Chauta, anthu amene Chauta waŵasankha akeake. Chauta ali kumwamba, amayang'ana pansi ndi kuwona anthu onse. Kumene amakhala pa mpando wachifumuko, amapenya anthu onse okhala pa dziko lapansi Amene amapanga mitima ya anthu onse, ndiye amene amapenya ntchito zao zonse. Mfumu siipulumuka chifukwa cha kukula kwa gulu lake la ankhondo. Wankhondo sapulumuka chifukwa chakuti ali ndi mphamvu zambiri. Pa kavalo wankhondo sungaikepo mtima kuti upambane, chifukwa sangathe kupulumutsa munthu, ngakhale kavaloyo ali ndi mphamvu zambiri. Chauta amayang'ana anthu omumvera, ndi odalira chikondi chake chosasinthika. Iye amachita izi kuti aŵapulumutse ku imfa ndi kuŵasungira moyo anthuwo pa nthaŵi ya njala. Mitima yathu ikuyembekeza Chauta, chifukwa Iye ndiye chithandizo ndi chishango chathu. Mitima yathu imasangalala mwa Chauta, popeza kuti timadalira dzina lake loyera. Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu. Ndidzayamika Chauta nthaŵi zonse, pakamwa panga padzatamanda Iye kosalekeza. Moyo wanga umanyadira Chauta. Anthu ozunzika amve ndipo akondwere. Lalikani pamodzi nane ukulu wa Chauta, tiyeni limodzi tiyamike dzina lake. Ndidapemphera kwa Chauta ndipo adandiyankha. Adandipulumutsa kwa zonse zimene ndinkaziwopa. Ozunzikawo atayang'ana kwa Chauta, nkhope zao zidasangalala, sadachite manyazi. Munthu wosaukayu adalira, ndipo Chauta adamumva, nampulumutsa m'mavuto ake onse. Mngelo wa Chauta amatchinjiriza anthu omvera Iye, ndipo amaŵapulumutsa. Yesani ndipo mudzaona kuti Chauta ndi wabwino. Ngwodala munthu wothaŵira kwa Chauta. Muzimvera Chauta, inu anthu ake oyera mtima, pakuti amene amamumvera sasoŵa kanthu. Ngakhale anaamkango amasoŵa chakudya ndipo amakhala anjala, koma anthu amene amalakalaka Chauta, sasoŵa zinthu zabwino. Bwerani ana anga, mundimvere, ndidzakuphunzitsani kuwopa Chauta. Ndani mwa inu amakhumba moyo ndi kulakalaka kuti akhale masiku ambiri, kuti asangalale ndi zinthu zabwino? Ngati ufunadi moyo, usalankhule zoipa, pakamwa pako pasakambe zonyenga. Lewa zoipa, ndipo uchite zabwino. Funafuna mtendere ndi kuulondola. Ngati mumvera Chauta, adzakuyang'anirani ndipo adzayankha kupempha kwanu. Koma Chauta amaŵakwiyira anthu ochita zoipa, anthuwo sadzakumbukikanso pansi pano. Pamene anthu ake akulira kuti aŵathandize, Chauta amamva naŵapulumutsa m'mavuto ao onse. Chauta amakhala pafupi ndi anthu a mtima wosweka, amapulumutsa otaya mtima. Anthu a Mulungu amaona masautso ambiri. Komabe Chauta amawapulumutsa m'mavuto awo onse. Chauta amasunga thupi la munthuyo, palibe fupa limene limasweka. Choipa chitsata mwini, anthu odana ndi munthu wa Mulungu adzalangidwa. Chauta amaombola moyo wa atumiki ake. Palibe wothaŵira kwa Iye amene adzalangidwe. Inu Chauta, mulimbane nawo anthu olimbana nane, Mumenyane nawo omenyana nane. Gwirani chishango ndi lihawo, ndipo fulumirani mundithandize. Tengani mkondo ndi nthungo, kuti mulimbane nawo anthu ondilondola. Uzani mtima wanga kuti, “Mpulumutsi wako ndine.” Anyozeke ndi kuchita manyazi onse ofunafuna moyo wanga. Abwezeni m'mbuyo ndipo athaŵe chinambalala amene apangana kuti andichite choipa. Akhale ngati mankhusu ouluka ndi mphepo, pamene mngelo wa Chauta akuŵapirikitsa. Njira yao ikhale yamdima ndi yoterera, pamene mngelo wa Chauta akuŵalondola. Adaniwo adanditchera ukonde popanda chifukwa, adandikumbira mbuna ine munthu wosachimwa. Aonongeke pamene iwo sakuyembekeza. Akodwe mu ukonde wotcha okha, agwere m'mbuna yokumba iwo omwe. Motero mtima wanga udzakondwa motamanda Chauta, kukondwerera kuti wandipulumutsa. Ndidzasangalala ndi mtima wonse ndi kunena kuti. “Ndani angafanefane ndi Inu Chauta, Inu amene mumapulumutsa munthu wofooka kwa munthu wopambana pa mphamvu, Inu amene mumapulumutsa munthu wofooka ndi wosoŵa kwa munthu wolanda zinthu zake?” Mboni zoipa zikundiwukira, zikundifunsa zinthu zimene sindikuzidziŵa. Zikundibwezera zoipa pa zabwino, ndipo mtima wanga uli ndi chisoni chokhachokha. Koma ine pamene adani anga analikudwala, ndidavala chiguduli kuwonetsa chisoni. Ndidadzilanga posala zakudya. Ndidapemphera nditaŵeramitsa mutu wanga pa chifuŵa, monga ngati ndikuchitira chisoni bwenzi langa kapena mbale wanga. Ndinkayenda khumakhuma ngati munthu wolira maliro a mai wake, nditaŵerama ndi kumalira. Koma ine nditagwa m'mavuto, iwo aja adasonkhana akusangalala. Adandisonkhanira onse pamodzi, anthu achabechabe amene sindidaŵadziŵe nkomwe, ndipo ankangondisinjirira. Anthuwo ankapitirira kundinyodola mwachipongwe, namandikukutira mano ao. Inu Chauta, mudzakhala mpaka liti mukungoyang'ana? Landitseni kwa anthu ofuna kundiwononga, mupulumutse moyo wanga ku mikangoyi. Tsono ndidzakuthokozani pa msonkhano waukulu, ndidzakutamandani pa chinamtindi cha anthu anu. Musalole kuti adani anga onyenga akondwere chifukwa cha mavuto anga, musalole kuti amene amandida popanda chifukwa, andiyang'ane cham'mbali mondinyoza. Iwo salankhula za mtendere, koma amangoganiza zonamizira okonda za mtendere pa dziko. Amandiseka mofuula namanena kuti, “Ha! Maso athu apenyadi zimene zidachitikazo.” Inu Chauta, amene mwaona zimenezi, musakhale chete. Musakhale kutali ndi ine, Inu Ambuye. Tiyeni, Inu Chauta, dzukani kuti munditchinjirize pa mlandu wanga, Inu Mulungu wanga ndi Ambuye anga. Chauta, Mulungu wanga, chifukwa cha kulungama kwanu, onetsani kuti ine ndine wosalakwa, ndipo musalole kuti adani anga akondwere chifukwa cha mavuto anga. Musalole kuti mumtima mwao anene kuti, “Inde, ndizo zimene timafuna.” Asanene kuti, “Tamgonjetsa.” Amene amakondwera poona kuti ndili pa mavuto, muŵachititse manyazi, muŵasokoneze kwathunthu. Amene amayesa kuti akupambana ine, achite manyazi ndipo anyozeke. Koma amene amafunitsitsa kuti ndipezeke wosalakwa, afuule ndi chimwemwe ndipo asangalale. Anene nthaŵi zonse kuti, “Chauta ndi wamkulu. Amakondwera akaona mtumiki wake zamuyendera bwino.” Tsono nanenso ndidzalalika za kulungama kwanu. Ndidzakutamandani masiku onse, Inu Chauta. Uchimo umalankhula mu mtima wa munthu wosamvera Mulungu. Alibe mantha ndi Mulungu m'maganizo mwake. Amadzinyenga m'maganizo mwake, kotero kuti tchimo lake sangathe kulizindikira ndi kudana nalo. Mau a pakamwa pake ndi oipa ndi onyenga. Sachita zanzeru kapena zabwino. Amaganiza zachiwembu akamagona usiku. Amayenda pa njira imene siili yabwino, sapewa zoipa. Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chimafika mpaka kumwamba, kukhulupirika kwanu kumafika mpaka ku mitambo. Kulungama kwanu kumaonekera ngati mapiri aatali, kuweruza kwanu nkozama ngati nyanja yakuya, Inu Chauta, mumasamalira anthu ndi nyama zomwe. Chikondi chanu chosasinthika ndi chamtengowapatali. Nchifukwa chake anthu anu amathaŵira m'munsi mwa mapiko anu. Mumaŵadyetsa zonona m'nyumba mwanu, ndipo mumaŵamwetsa madzi a mu mtsinje wa madalitso anu. Kwa Inu kuli kasupe wamoyodi, m'kuŵala kwanu ifenso timaona kuŵala. Musaleke kuŵakonda ndi chikondi chanu chosasinthika anthu okudziŵani, pitirizani kuŵachitira zokoma anthu olungama mtima. Musalole kuti mapazi a anthu odzikuza andipondereze, ndipo kuti manja a anthu oipa andipirikitse. Onani, ochita zoipa ali ngundangunda. Inu mwaŵagwetsa pansi ndipo sangathe kudzuka. Usamavutika ndi anthu oipa. Usamakhumbira kukhala ngati ochita zoipa, pakuti mosachedwa amanyala ngati udzu, ndipo amafota ngati masamba aaŵisi. Khulupirira Chauta ndipo uzichita zabwino. Khala m'dziko ndi kutsata zokhulupirika. Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba. Udzipereke m'manja mwa Chauta, umukhulupirire ndipo Iye adzakusamalira. Adzaonetsa poyera kusalakwa kwako, ndipo kulungama kwako kudzaŵala ngati usana. Khala bata pamaso pa Chauta, ndipo umdikire mosadandaula. Usavutike ndi munthu amene zake zikumuyendera bwino, ndi munthu amene amatha kuchitadi zoipa zimene wakonza. Lewa kupsa mtima ndi kukwiya. Usachite zimenezi, pakuti sudzapindula nazo kanthu. Pajatu anthu oipa adzaonongeka, koma okhulupirira Chauta adzalandira dziko kuti likhale lao. Kanthaŵi pang'ono ndipo munthu woipa sadzakhalaponso, ngakhale muyang'ane bwino pamalo pamene analiri, simudzampezapo. Koma anthu ofatsa adzalandira dziko kuti likhale lao, ndipo adzakhala pa mtendere wosaneneka. Munthu woipa amachitira upo mnzake wabwino, namamtuzulira maso mwachidani. Koma Chauta amamseka munthu woipayo, poti amaona kuti tsiku lake la kuwonongeka likubwera. Anthu oipa amasolola lupanga, ndipo amakoka mauta, kuti aphe anthu ovutika ndi osoŵa, amene amayenda molungama. Koma lupanga lao lidzalasa mitima ya eniake omwewo, ndipo mauta ao adzaŵathyokera m'manja. Nkwabwino kukhala m'chilungamo ndi kusauka, kupambana kukhala nazo zokoma zambiri zimene munthu woipa ali nazo. Pakuti Chauta adzathetsa mphamvu za anthu oipa, koma adzalimbikitsa anthu onse abwino. Chauta amasamalira moyo wa anthu angwiro, ndipo choloŵa chao chidzakhalapo mpaka muyaya. Pa nthaŵi ya mavuto sadzazunzika, pa nthaŵi yanjala, adzakhala nazo zakudya zochuluka. Koma anthu oipa amatha. Adani a Chauta amafota ngati maluŵa, amazimirira ngati utsi. Munthu woipa amakonda ngongole koma satha kubweza, koma munthu wabwino ali ndi mtima wokoma ndi wopatsa. Anthu amene Chauta adaŵadalitsa, adzalandira dziko kuti likhale lao, koma amene Chauta adaŵatemberera adzaonongeka. Chauta amatsogolera mayendedwe a munthu wolungama, amatchinjiriza amene njira zake zimakomera Iye. Ngakhale agwe sadzapweteka, popeza kuti Chauta amamgwira dzanja. Chiyambire unyamata wanga mpaka ukalamba wanga uno, sindidaonepo munthu wabwino atasiyidwa ndi Mulungu, kapena ana ake akupempha chakudya. Nthaŵi zonse munthu wolungama amapatsa mosaumira, ndipo amakongoza mwaufulu, ana ake amakhala madalitso. Tsono leka zoipa, ndipo chita zabwino, motero udzakhala pa mtendere mpaka muyaya. Chauta amakonda chilungamo, sadzaŵasiya okha anthu ake okhulupirika. Iye adzawasunga mpaka muyaya, koma adzaononga ana a anthu oipa. Anthu a Mulungu adzalandira dziko kuti likhale lao, ndipo adzakhala m'menemo mpaka muyaya. Munthu wabwino amalankhula zanzeru, pakamwa pake pamatuluka zachilungamo. Malamulo a Mulungu amakhala mumtima mwake, motero sagwedezeka poyenda m'moyo uno. Munthu woipa amazonda munthu wabwino, amafunafuna kuti amuphe. Koma wolungamayo Chauta sadzamsiya yekha m'manja mwa mdani wake, sadzalola kuti pomuweruza, mlandu wake umuipire. Khulupirira Chauta, ndipo usunge njira zake. Motero adzakukweza ndipo udzalandira dziko kuti likhale lako. Udzaona anthu oipa akuwonongeka. Ndidaona munthu woipa akunyada ndi kudzitukumula ngati mkungudza wa ku Lebanoni. Koma pambuyo pake, podutsanso, ndidaona kuti palibe. Ngakhale ndidamfunafuna, sindidathe kumpeza. Upenye munthu wopanda cholakwa ndi wolungama, ndipo udzapeza kuti munthu wamtendere ali ndi zidzukulu zambiri. Koma anthu ochimwa adzaonongekeratu kwathunthu, iwo pamodzi ndi zidzukulu zao zomwe. Chipulumutso cha anthu abwino chimachokera kwa Chauta. Chauta ndiye kothaŵirako anthuwo pa nthaŵi yamavuto. Chauta amaŵathandiza ndi kuŵalanditsa. Amaŵachotsa m'manja mwa anthu oipa nkuŵapulumutsa, popeza kuti anthuwo amadalira Iye. Inu Chauta musandikwiyire ndi kundidzudzula. Musapse mtima ndi kundilanga. Mivi yanu yandilasa, ndipo dzanja lanu landipsinja. Thupi langa lilibe mphamvu chifukwa cha ukali wanu. M'nkhongono mwanga mwalobodoka chifukwa cha uchimo wanga. Machimo anga andimiza msinkhu, akundilemera ngati katundu woposa mphamvu zanga. Mabala anga aola ndipo akununkha chifukwa cha kupusa kwanga. Ndapindika msana kwathunthu, ndaŵerama zedi, ndatha mphamvu, tsiku lonse ndimangonka ndilira. Thupi langa likutentha kwambiri ndi malungo, ndipo lilibe nyonga. Ndatheratu, ndipo ndatswanyika. Ndikubuula chifukwa cha kuvutika mu mtima. Ambuye, mumadziŵa zonse zimene ndimakhumba, kusisima kwanga sikuli kosamveka kwa Inu. Mtima wanga ukugunda, mphamvu zandithera, ndipo sindikutha kupenya bwino. Abwenzi anga ndi anzanga omwe amandiimira kutali, chifukwa cha matenda anga. Achibale anga nawonso amandipewa. Anthu ofunafuna moyo wanga, amanditchera misampha. Ofuna kundipweteka amalankhula zondiwononga, tsiku lonse amangolingalira zondichita chiwembu. Koma ine ndili ngati gonthi, sindikumvako, ndili ngati mbeŵeŵe amene satha kulankhula. Inde ndili ngati munthu amene saamva, chifukwa sindingathe kuyankhapo kanthu, pamene akundilankhula. Koma tsono ndimayembekezera Inu Chauta, Ndinu Chauta, Mulungu wanga amene mudzayankha. Popeza ndimapemphera kuti, “Musalole konse kuti akondwerere pa ine, amene amandinyodola akaona kuti ndikuterereka.” Inde, ndili pafupi kugwa, ndipo ndikumva kuŵaŵa nthaŵi zonse. Ndikuvomera kuipa kwanga, ndikuda nkhaŵa chifukwa cha machimo anga. Ngamphamvu adani amene amafuna moyo wanga, ngambiri amene amandida popanda chifukwa. Anthu amene amandibwezera zoipa m'malo mwa zabwino ndiwo adani anga, chifukwa ine ndimachita zabwino. Musandisiye ndekha, Inu Chauta, Inu Mulungu wanga, musakhale nane kutali. Fulumirani kudzandithandiza, Inu Ambuye, Mpulumutsi wanga. Ndidati, “Ndidzasamala zochita zanga, kuti ndisachimwe polankhula. Ndidzatseka pakamwa panga nthaŵi zonse pamene anthu oipa ali nane.” Motero ndidakhala chete osalankhula kanthu, ndidakhala duu, koma popanda phindu, chifukwa mavuto anga ankangokulirakulira. Mtima wanga udavutika, ndipo pamene ndidasinkhasinkha, mtima wanga udangoyaka moto. Pompo ndidalankhula ndi mau akuti, “Inu Chauta, mundidziŵitse mathero a moyo wanga, mundidziŵitse kuchepa kwa masiku anga. Mundilangize kuti moyo wanga sukhalira kutha. “Onani, mwandipatsa masiku ochepa chabe, nthaŵi ya moyo wanga siili kanthu pamaso panu. Ndithudi, munthu aliyense ndi mpweya chabe. Zoonadi, munthu amayenda ngati chithunzithunzi, amangovutika ndi zachabechabe. Munthu amakundika chuma, koma amene adzachidye ndi wosadziŵika. “Nanga tsopano, Inu Ambuye, ndikudikira chiyani? Chikhulupiriro changa chili pa Inu. Pulumutseni ku zolakwa zanga zonse. Musandisandutse chinthu chochinyodola zitsiru. Ndine mbeŵeŵe, sinditsekula pakamwa panga, pakuti ndinu amene mwachita zimenezi. “Chotsani chikoti chanu pa ine, ndatheratu chifukwa cha mkwapulo wanu. Inu mumalanga munthu pakumdzudzula chifukwa cha uchimo wake. Mumaonongeratu zimene iye amazikonda, monga m'mene chimachitira chifukufuku. Zoonadi, munthu aliyense ndi mpweya chabe. “Mverani pemphero langa, Inu Chauta, mumve kulira kwanga. Musakhale chete pamene ndikulirira Inu. Ndine mlendo wanu wosakhalitsa, munthu wongokhala nawo monga adaachitira makolo anga onse. Musandiyang'ane mwaukali, choncho ndidzatha kusangalala, ndisanafe ndi kuzimirira.” Ine ndidayembekeza Chauta ndi mtima wokhulupirira kuti adzandithandize. Adaŵeramira pansi kuyang'ana kwa ine, namva kulira kwanga. Adanditulutsa m'dzenje la chiwonongeko, m'chithaphwi chamatope. Adapondetsa mapazi anga pa thanthwe, nandiyendetsa bwino lomwe. Mulungu waika nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, nyimbo yake yotamanda Iye. Anthu ambiri adzaona zimenezi ndipo adzaopa, nadzakhulupirira Chauta. Ngwodala munthu amene amadalira Chauta, munthu amene sapatukira ku mafano kapena kutsata milungu yonama. Inu Chauta, Mulungu wanga, mwatichitira zodabwitsa zambiri, mwatikonzera zabwino zambiri zakutsogolo. Palibe ndi mmodzi yemwe wotha kulingana nanu. Ndikati ndisimbe ndi kulongosola za zimenezo, sindingathe kuziŵerenga zonse chifukwa cha kuchuluka kwake. Simudafune nsembe ndi zopereka, koma mwandipatsa makutu oti ndizimvera. Simudapemphe nsembe yopsereza ndi yopepesera machimo. Tsono ndidati, “Ndilipo, ndikubwera, monga zidalembedwa za ine m'buku la malamulo. Ndimakonda kuchita zimene mumafuna, Inu Mulungu wanga, malamulo anu ali mumtima mwanga.” Ndalalika uthenga wabwino wa chipulumutso chanu pa msonkhano waukulu. Sindidatseke pakamwa, monga mukudziŵa, Inu Chauta. Sindidabise mumtima mwanga zoti ndinu wolungama. Ndalankhula za kukhulupirika kwanu ndi za chipulumutso chanu. Sindidaŵabisire a pa msonkhano waukulu za chikondi chanu chosasinthika ndi za kukhulupirika kwanu. Musandichotsere chifundo chanu, Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika ndi kukhulupirika kwanu zindisunge nthaŵi zonse. Mavuto osaŵerengeka andizinga, machimo anga andigwira, kotero kuti sindingathe kuwona populumukira, ngambiri kupambana tsitsi la kumutu kwanga, ndipo ndataya mtima kotheratu. Inu Chauta, pulumutseni. Inu Chauta, fulumirani kudzandithandiza. Anthu ofunafuna moyo wanga, muŵachititse manyazi ndi kuŵasokoneza. Okhumba kundipweteka, abwezedwe m'mbuyo ndi kunyozedwa. Amene amandinyodola kuti, “Ha, Ha,” achoke ndi kuchita manyazi poona kuti alephera. Koma onse okufunafunani akondwe ndi kusangalala chifukwa cha Inu. Onse okondwerera chipulumutso chanu azinena kosalekeza kuti, “Chauta ndi wamkulu!” Inu Chauta, ine ndine wolefuka ndi wosoŵa, koma simunandiiŵale. Inu ndinu mthandizi wanga ndi Mpulumutsi wanga. Inu Mulungu wanga, musachedwe kudzandithandiza. Ngwodala munthu amene amaganizirako za amphaŵi, popeza kuti Chauta adzapulumutsa munthu wotere pa tsiku lamavuto. Chauta adzamteteza ndi kumsunga ndi moyo. Adzatchedwa wodala pa dziko. Chauta sadzampereka kwa adani ake, kuti amchite zimene iwo akufuna. Chauta adzamthandiza munthuyo akamadwala. Adzamchiritsa matenda ake onse. Tsono ndidati, “Inu Chauta, ndakuchimwirani, mundikomere mtima, muchiritse moyo wanga.” Koma adani anga ondifunira zoipa, amati, “Kodi munthu ameneyu adzafa liti, kuti aiŵalike?” Amene amabwera kudzandiwona, ndi wosakhulupirika, mumtima mwake amaganiza zoipa za ine, ndipo akatuluka, amakaziwanditsa. Onse odana nane amanong'onezana za ine, amayesa kuti zoipa zandigwera chifukwa cha kuipa kwanga. Amati, “Yamgwera nthenda yofa nayo, sadzukanso pamene wagonapo.” Ngakhalenso bwenzi langa lapamtima amene ndinkamkhulupirira, amene ankadya nane pamodzi, wandiwukira. Koma Inu Chauta, mundikomere mtima, mundichiritse kuti ndiŵalange anthuwo. Mukatero ndidzadziŵa kuti mumakondwera nane, chifukwa mdani wanga sadandipambane. Inu mwandichirikiza chifukwa cha kukhulupirika kwanga, mwandikhazika pamaso panu mpaka muyaya. Atamandike Chauta, Mulungu wa Israele, kuyambira muyaya mpaka muyaya. Inde momwemo. Inde momwemo. Monga momwe mbaŵala imakhumbira mtsinje wamadzi, ndimo m'mene mtima wanga umakhumbira Inu Mulungu wanga. Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Mulungu, Mulungu wamoyo. Kodi ndidzafika liti pamaso pa Mulungu? Ntchito yanga ndi kulira usana ndi usiku, osalaŵa chakudya chilichonse. Ndipo anthu akhala akunena kuti, “Mulungu wako ali kuti?” Mtima wanga umaŵawa ndikamakumbukira m'mene ndinkayendera ndi chinamtindi cha anthu, poŵatsogolera ku Nyumba ya Mulungu. Panali khwimbi la anthu ofuula mosangalala, akuimba nyimbo zothokoza ndipo akuchita chikondwerero. Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika choncho m'kati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamtamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga. Ndatayiratu mtima, nchifukwa chake ndikukumbukira Inu Mulungu, pamene ndili ku dziko la Yordani, ku Heremoni ndi ku phiri la Mizara. Madzi akuya akuitanizana ndi madzi akuyanso, mathithi anu akulindima kochititsa mantha. Mafunde anu ang'onoang'ono ndi akuluakulu omwe andimiza. Komabe Chauta amaonetsa chikondi chake chosasinthika tsiku ndi tsiku, Nchifukwa chake nthaŵi zonse ndimamuimbira nyimbo, ndi kumpemphera Mulungu wondipatsa moyo. Ndimafunsa Mulungu, thanthwe langa, kuti, “Mwandiiŵaliranji? Ndiziyenderanji ndilikulira chifukwa chondipsinja mdani wanga?” Kunyoza kwa adani anga kumandipweteka ngati bala lofa nalo la m'thupi mwanga, akamandifunsa nthaŵi zonse kuti, “Mulungu wako ali kuti?” Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika choncho m'kati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamtamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga. Inu Mulungu, onetsani kuti ine ndine wosalakwa, munditchinjirize pa mlandu wanga kwa anthu osasamala za Mulungu. Mundipulumutse kwa anthu onyenga ndi opanda chilungamo. Ndithu Inu ndinu Mulungu wamphamvu amene ndimathaŵirako. Mwanditayiranji? Ndiziyenderanji ndilikulira chifukwa chondipsinja mdani wanga? Tumizani kuŵala kwanu ndi choona chanu kuti zinditsogolere. Zindifikitse ku phiri lanu loyera, kumalo kokhala Inu. Tsono ndidzapita ku guwa lansembe la Mulungu, kwa Mulungu amene amandipatsa chimwemwe chopambana. Ndipo ndidzakutamandani ndi pangwe, Inu Mulungu, Mulungu wanga. Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika choncho m'kati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamtamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga. Inu Mulungu, ife tidamva ndi makutu athu, makolo athu adatiwuza za ntchito zimene mudagwira pa masiku ao, masiku amakedzana. Inu mudapirikitsa mitundu ina ya anthu, koma makolo athu mudaŵakhazika m'dziko lao. Inu mudasautsa mitundu ina ya anthu, koma makolo athuwo Inu mudaŵapatsa ufulu. Iwo sadalande dziko ndi lupanga lao, sadapambane pa nkhondo ndi mphamvu zao. Koma adagonjetsa ndi mphamvu zanu, chifukwa cha kuŵala kwa nkhope yanu, pakuti mudakondwera nawodi. Inu ndinu Mfumu yanga ndi Mulungu wanga, amene mudampambanitsa Yakobe pa nkhondo. Ndi thandizo lanu tidakantha adani athu. Ndi mphamvu zanu tidapondereza ogalukira. Sindidalira uta wanga, ngakhale lupanga langa silingandipulumutse. Koma Inu mwandilanditsa kwa adani athu, mwaŵachititsa manyazi amene amadana nafe. Takhala tikunyadira mphamvu za Mulungu nthaŵi zonse, ndipo tidzakuthokozani mpaka muyaya. Komabe Inu mwatitaya, ndipo mwatitsitsa, simunapite nawo limodzi ankhondo athu. Mwalola kuti amaliwongo athu atipirikitse, ndipo adani athu apeza zofunkha kwathu. Inu mwatisandutsa nkhosa zokaphedwa, mwatibalalitsa pakati pa mitundu ina ya anthu. Inu mwagulitsa anthu anu pa mtengo wotsika, ndipo simudapindulepo kanthu ai. Inu mwatisandutsa anthu onyozeka kwa anzathu oyandikana nafe, anthu otizungulira amatiseka ndi kutinyodola. Inu mwatisandutsa anthu oŵanyodola pakati pa anthu a mitundu ina, anthu omangosekedwa pakati pa anzathu. Tsiku lonse ndimangodziwona kuti ndine munthu wopandapake. Nkhope yanga yagwa chifukwa cha manyazi, pakumva mau a anthu onditonza ndi onditukwana, poona mdani wanga ndi munthu wolipsira. Zonsezi zatigwera, ngakhale kuti sitidakuiŵaleni ndipo sitidaphwanye chipangano chanu. Mtima wathu sudabwerere m'mbuyo, mapazi athu sadaleke kuyenda m'njira yanu. Komabe Inuyo mwatitswanya ndi kutisiya pakati pa nkhandwe ku chipululu, kumene kuli mdima wandiweyani. Tikadaiŵala Mulungu wathu, kapena kugwadira mulungu wachilendo, kodi Mulungu sakadazipeza zimenezi? Paja Iye amadziŵa zinsinsi zonse zamumtima. Koma chifukwa cha Inu, adani akutipha tsiku lonse, pamaso pao tili ngati nkhosa zimene akukazipha. Dzukani, Inu Ambuye. Chifukwa chiyani mukukhala ngati mwagona? Khalani maso, musatitaye kotheratu. Chifukwa chiyani mwatifulatira? Mwaiŵaliranji masautso athu ndi kupsinjidwa kwathu? Ife tagwa pansi m'fumbi, thupi lathu langoti thapsa pa dothi. Dzukani, mubwere kudzatithandiza. Tiwomboleni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika. Mtima wanga wadzaza ndi nkhani yokoma. Ndikuimbira mfumu nyimbo yangayi. Lilime langa lili ngati cholembera cha katswiri wodziŵa kulemba bwino. Inu ndinu wokongola kwambiri kuposa anzanu ena onse. Pakamwa panu pamatulutsa zokoma zokhazokha. Nchifukwa chake Mulungu wakudalitsani mpaka muyaya. Inu ngwazi yolimba mtima, mangirirani lupanga lanu m'chiwuno, mu ulemerero ndi ukulu wanu. Pitani ndi ulemerero wanuwo, kuti mukagonjetse adani anu onse, mukateteze zimene zili zoona, zachifatso ndi zachilungamo. Dzanja lanu lamanja likaonetse ntchito zanu zoopsa. Mivi yanu ndi yakuthwa, imalasa mitima ya adani. Mitundu ina ya anthu imagwa pansi pamaso panu. Mpando wanu waufumu, Inu Mulungu, ndi wamuyaya, mumaweruza molungama mu ufumu wanu. Mumakonda chilungamo ndipo mumadana ndi zoipa. Nchifukwa chake Mulungu, Mulungu wanu, wakusankhani. Wakudzozani ndi kukusangalatsani kupambana anzanu ena onse. Zovala zanu nzonunkhira mure, aloe ndi kasiya. Nyumba zanu zachifumu nzomangidwa ndi mnyanga. M'menemo zoimbira zansambo zimakusangalatsani, ana aakazi a mafumu ali m'gulu la mbumba zanu zolemekezeka. Ku dzanja lanu lamanja kwaima mfumukazi, yovala zovala za golide wa ku Ofiri. Tsono mvera kuno, mkwati wamkaziwe, imva mau anga ndipo uŵaganizire bwino. Iŵala abale ako ndiponso nyumba ya bambo wako. Mfumu idzakukonda chifukwa cha kukongola kwako. Umuŵeramire popeza kuti ndiye mbuyako. Anthu a ku Tiro adzakukopa ndi mphatso, olemera kwambiri adzakunyengerera ndi chuma chao chamitundumitundu. Mwana wamkazi wa mfumu ali m'chipinda mwake, wadzikongoletsa kwambiri, wavala zovala zoluka ndi thonje lagolide. Akupita naye kwa mfumu atavala zovala zamaluŵa, pamodzi ndi anamwali anzake omperekeza. Akuŵaperekeza ndi chimwemwe ndi chisangalalo pokaloŵa m'nyumba ya mfumu. Inutu zidzukulu zanu zidzaloŵa m'malo mwa makolo anu, mudzaŵasandutsa mafumu pa dziko lonse lapansi. Ndidzamveketsa mbiri ku mibadwo yonse, nchifukwa chake mitundu ya anthu idzakutamandani mpaka muyaya. Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto. Nchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisinthike, ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja zozama, ngakhale nyanja zikokome ndi kututuma. Ngakhale mapiri anjenjemere ndi kulindima kwa nyanja. Koma kuli mtsinje umene mifuleni yake imasangalatsa anthu amumzinda wa Mulungu, malo oyera okhalako Wopambanazonse. Mulungu ali m'kati mwa mzindawo, sudzaonongeka konse. Mulungu adzauthandiza dzuŵa lisanatuluke. Mitundu ya anthu ikunjenjemera kwambiri, maufumu akugwedezeka, Mulungu akalankhula mau ake, dziko lapansi likusungunuka. Chauta Wamphamvuzonse ali nafe. Mulungu wa Yakobe ndiye kothaŵira kwathu. Bwerani kuti muwone ntchito za Chauta, m'mene amachitira zozizwitsa pa dziko lapansi. Amaletsa nkhondo mpaka ku mathero a dziko lapansi. Amathyola uta, ndi kupokonyola mkondo. Amatentha magaleta ankhondo ndi moto. “Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.” Chauta Wamphamvuzonse ali nafe, Mulungu wa Yakobe ndiye kothaŵira kwathu. Ombani m'manja inu anthu a mitundu yonse. Fuulani kwa Mulungu poimba nyimbo zachimwemwe. Paja Chauta Wopambanazonse, ndi woopsa, ndiye mfumu yaikulu pa dziko lonse lapansi. Iye adatigonjetsera anthu ambirimbiri, mitundu ina ya anthu adaiika pansi pa ulamuliro wathu. Adatisankhulira dzikoli kuti likhale choloŵa chathu, adatipatsa ife anthu a Yakobe dziko lokomali pakuti amatikonda. Mulungu wakwera, anthu akumfuulira, Chauta wakwera, akumuimbira lipenga. Imbani nyimbo zotamanda Mulungu, imbani nyimbo zotamanda. Imbani nyimbo zotamanda mfumu yathu, imbani nyimbo zotamanda. Mulungu ndiye Mfumu ya dziko lonse lapansi. Imbani mwaluso nyimbo zotamanda. Mulungu amalamulira mitundu ya anthu. Mulungu amakhala pa mpando wake woyera waufumu. Atsogoleri a anthu a mitundu ina yonse amasonkhana pamodzi ndi anthu a Mulungu wa Abrahamu, pakuti mafumu onse a pansi pano ndi ake a Mulungu, Iyeyo ndiye wamkulu kopambana. Chauta ndi wamkulu, ndi woyenera kumutamanda kwambiri. Timuyamike mu mzinda wake, pa phiri lake loyera, mzinda wokongola wa Ziyoni pa phiri la Mulungu, wopatsa chimwemwe ku dziko lonse lapansi. Mzinda wa Ziyoni umene uli kumpotowu, ndi mzinda wa Mfumu yathu yaikulu. Mulungu waonetsa kuti ndiye woteteza mzindawo, pakuti Iye amakhala m'kati mwa malinga ake. Mafumu adasonkhana, adafuna kuuthira nkhondo pamodzi. Atangopenya mzindawo adadzidzimuka, adachita mantha, nathaŵa chinambalala. Adanjenjemera koopsa, ndipo adamva ululu wonga wa mkazi wovutika pa nthaŵi yochira. Inu Mulungu mudaŵaononga, monga momwe mphepo yakuvuma ija imapasulira zombo zopita ku Tarisisi. Zimene ife tidazimva, taziwona zomwezo mu mzinda wa Chauta Wamphamvuzonse, mzinda wa Mulungu wathu, umene adaukhazikitsa mpaka muyaya. Tikakhala m'Nyumba mwanu, Inu Mulungu, timalingalira za chikondi chanu chosasinthika. Inu Mulungu, anthu amakutamandani ponseponse, monga dzina lanu latchuka pa dziko lonse lapansi. Dzanja lanu lamphamvu limapambana nthaŵi zonse. Anthu okhala mu Ziyoni akondwe. A ku Yuda asangalale chifukwa cha kaweruzidwe kanu kolungama. Zungulirani Ziyoni yense, inde zungulirani mzinda wonsewo, ndipo muŵerenge nsanja zake. Yang'anani bwino machemba ake, penyetsetsani malinga ake, kuti mudzathe kusimbira mbadwo wakutsogolo. Mudzati, “Mulungu wathu ndi wotere, ndi Mulungu wathu kuyambira muyaya mpaka muyaya. Iye adzakhala wotitsogolera nthaŵi zonse.” Imvani izi, inu anthu a mitundu yonse. Tcherani khutu, inu nonse okhala pa dziko lapansi, anthu otsika ndi okwera omwe, olemera ndi osauka omwe. Zosinkhasinkha za mtima wanga zidzakhala zakuya, ndipo ndidzalankhula zanzeru. Ndidzakupherani mwambi, ndidzamasulira tanthauzo lake poimba pangwe. Ndichitirenji mantha pa nthaŵi yamavuto pamene anthu ondizunza akundizinga. Anthu otero amangokhulupirira chuma chao, amanyada chifukwa ali ndi chuma chambiri. Zoonadi, palibe munthu amene angadziwombole, kapena kupatsa Mulungu mtengo wa moyo wake. Popeza kuti choombolera moyo wa munthu ndi chamtengowapatali, ndipo sangathe kuchikwanitsa, kuti azikhalabe ndi moyo mpaka muyaya osapita ku manda. Zoonadi, aliyense atha kuwona kuti ngakhale anthu anzeru amafa. Chimodzimodzi, anthu opusa ndi opulukira ayenera kufa ndi kusiyira ena chuma chao. Manda ao ndiye kwao mpaka muyaya, ndi malo odzakhalako pa mibadwo yonse, ngakhale akadali moyo ankatcha maiko maina ao. Ngakhale munthu akhale wolemera chotani, komabe adzafa chabe ngati nyama zakuthengo. Zimenezi ndizo zimene zimaŵagwera anthu amene ali ndi chikhulupiriro chopusa, ndiwo mathero ake a onse amene amatsata maganizo otere. Ayenera kupita ku dziko la akufa ngati nkhosa, ndipo imfa idzakhala mbusa wao. Anthu olungama adzaŵapambana. Adzatsika kulunjika ku manda, matupi ao adzaola, kwao kudzakhala kumanda. Koma Mulungu adzaombola moyo wanga ku ulamuliro wa manda, sindidzaopa, pakuti Iye adzandilandira. Usavutike munthu wina akamalemera, pamene chuma cha m'nyumba mwake chikukulirakulira. Chifukwa pamene munthuyu amwalira, sadzatengapo kanthu. Chuma chake sichidzapita naye limodzi. Ngakhale pamene munthuyo ali moyo, amadziyesa wodala, ndipo ngakhale atamandidwe pamene zinthu zikumuyendera bwino, adzafabe nkukakumana ndi makolo ake onse kumanda, kumene sadzaona kuŵala mpaka muyaya. Ngakhale munthu akhale wolemera chotani, komabe akasoŵa nzeru, adzafa chabe ngati nyama zakuthengo. Chauta, Mulungu Wamphamvu uja, akulankhula, akuitana anthu a ku dziko lonse lapansi, kuyambira kotulukira dzuŵa mpaka koloŵera kwake. Mulungu akuŵala atakhala m'Ziyoni, mzinda wake wokongola kotheratu. Mulungu wathu akubwera, sakhala chete. Patsogolo pake pali moto wonyeketsa, M'mbali mwake monse muli mkuntho wamphamvu. Amaitana zamumlengalenga ndi za pansi pano, kuti zichite umboni pamene akuweruza anthu ake. Iye akuti, “Sonkhanitsani pamaso panga, anthu anga okhulupirika, amene adachita chipangano ndi Ine popereka nsembe.” Zamumlengalenga zikulalika chilungamo cha Mulungu, pakuti Iye mwini ndiye muweruzi. “Imvani anthu anga, Ine ndidzalankhula. Ndidzapereka umboni wokutsutsani inu Aisraele. Ine ndine Mulungu, Mulungu wanu. “Sindikudzudzulani chifukwa cha nsembe zanu, popeza kuti mumapereka nsembe zanu zopsereza kwa Ine nthaŵi zonse. Ndithudi, sindilandira ng'ombe kapena mbuzi iliyonse ya m'makola anu. “Popeza kuti nyama iliyonse yam'nkhalango ndi yanga, pamodzi ndi nyama zonse zokhala ku mapiri ochuluka. Mbalame zonse zamumlengalenga, zamoyo zonse zoyenda ku thengo ndi zanga. “Ndikadakhala ndi njala sindikadakuuzani, pakuti dziko lonse ndi zonse zam'menemo, ndi zanga. Kodi ndimadya nyama yang'ombe kapena magazi ambuzi? “Koma perekani nsembe zanu zothokozera kwa Mulungu, ndipo muchite zimene mudalumbira kwa Wopambanazonse. Mupemphere kwa Ine pa tsiku lamavuto. Ine ndidzakupulumutsani, ndipo inu mudzandilemekeza.” Koma kwa munthu woipa Mulungu amati, “Ukuvutikiranji ndi kutchula malamulo anga? Bwanji pakamwa pako pakulankhula za chipangano changa? Iwe sufuna kulangizidwa, umaponya mau anga ku nkhongo. “Ukaona mbala umasanduka bwenzi lake, ndipo umayenda ndi anthu achigololo. Suwopa kulankhula zoipa pakamwa pako, lilime lako limapeka mabodza. “Umakhala pansi nkumachitira mbale wako miseche, inde, umasinjirira mbale wako weniweni. Iwe wachita zinthu zimenezi, ndipo Ine ndakhala ndili chete. Unalikuganiza kuti ndimafanafana nawe. Koma tsopano ndikukudzudzula ndi kukuwonetsa zimene wachita. “Ganizani bwino izi tsono, inu amene mumaiŵala Mulungu, kuti ndingakukadzuleni, ndipo palibe amene angakupulumutseni. Koma wopereka mtima wake kwa Ine mothokoza, ndiye amene amandilemekeza. Woyenda m'njira zolungama, ndidzamuwonetsa chipulumutso changa.” Mundichitire chifundo, Inu Mulungu, malinga ndi chikondi chanu chosasinthika. Mufafanize machimo anga, malinga ndi chifundo chanu chachikulu. Mundisambitse kwathunthu pochotsa kulakwa kwanga, mundiyeretse mtima pochotsa machimo anga. Zolakwa zanga ndikuzidziŵa, kuchimwa kwanga ndikukuzindikira nthaŵi zonse. Ndachimwira Inu, Inu nokha, ndachita choipa pamaso panu. Motero mwakhoza ponditchula wolakwa, simudalakwe pogamula mlandu wanga. Zoonadi, ndidabadwa mu uchimo, ndinali mu uchimo kuyambira pamene mai wanga adatenga pathupi pa ine. Ndithudi, Inu mumakonda mtima woona, choncho mundiphunzitse nzeru zanu. Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzakhala woyera. Mundisambitse, ndipo ndidzayera kupambana chisanu chambee. Mundilole ndimve chimwemwe ndi chikondwerero. Ngakhale mwandiphwanyaphwanya mafupa, mundilole ndidzasangalalenso. Mufulatire machimo anga, mufafanize zoipa zanga zonse. Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika. Musandipirikitse pamaso panu, musachotse Mzimu wanu woyera mwa ine. Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu, mulimbitse mwa ine mtima womvera. Pamenepo ochimwa ndidzaŵaphunzitsa njira zanu, ndipo iwo adzabwerera kwa Inu. Mundikhululukire mlandu wanga wokhetsa magazi, Inu Mulungu, Mulungu Mpulumutsi wanga, ndipo ndidzakweza mau poimba za chipulumutso chanu. Ambuye, tsekulani milomo yanga, ndipo pakamwa panga padzalankhula zotamanda Inu. Si nsembe wamba imene Inu imakusangalatsani. Ndikadapereka nsembe yopsereza, sibwenzi Inu mutakondwera nayo. Nsembe imene Inu Mulungu mumailandira, ndi mtima wotswanyika. Mtima wachisoni ndi wolapa, Inu Mulungu simudzaunyoza. Muŵachitire zabwino anthu a ku Ziyoni, chifukwa cha kukoma mtima kwanu. Mumangenso kachiŵiri makoma a Yerusalemu. Pamenepo mudzakondwera ndi nsembe zoyenera, nsembe zootcha ndi zopsereza kwathunthu. Choncho adzapereka ng'ombe zamphongo pa guwa lanu lansembe. Bwanji ukunyadira ntchito zako zoipa, munthu wamphamvuwe? Tsiku lonse umakhalira kusinkhasinkha za kuwononga ena, lilime lako lili ngati lumo lakuthwa, ntchito yako nkunyenga. Umakonda zoipa kupambana zabwino, umakonda kunama kupambana kulankhula zoona. Umakonda kulankhula mau ovutitsa ena, iwe wabodzawe. Koma Mulungu adzakutswanya kosalekeza, adzakugwira ndi kukutulutsira kunja kwa nyumba yako. Adzakuzula m'dziko la anthu amoyo. Anthu ochita zachilungamo adzaona zimenezi, ndipo adzachita mantha. Adzakuseka ndi kumanena kuti, “Muwoneni munthu amene sadafune kudalira Mulungu, koma adakhulupirira chuma chake chochuluka, nalimbikira kuchita zoipa.” Koma ine ndili ngati mtengo wauŵisi wa olivi m'Nyumba ya Mulungu. Ndimaika mtima nthaŵi zonse pa chikondi chosasinthika cha Mulungu. Ndidzakuthokozani Inu Mulungu mpaka muyaya, chifukwa cha zimene mwachita. Ndidzatamanda dzina lanu pamaso pa anthu okukondani, pakuti ndinu abwino. Mumtima mwake munthu wopusa amati, “Kulibe Mulungu.” Anthu otereŵa ndi oipa, amachita zonyansa, palibe ndi mmodzi yemwe wochita zabwino. Mulungu kumwambako waŵerama, akuyang'ana anthu pansi pano, kuti aone ngati angakhalepo mmodzi wanzeru wofunitsitsa Mulungu. Koma ai anthu onse ndi osokera, onsewo ndi oipa chimodzimodzi. Palibe ndi mmodzi yemwe wochita zabwino, ai, palibiretu ndi mmodzi yemwe. Kani anthu oipaŵa alibe nzeru chotere? Iwo amameza anthu anga, kuŵayesa chakudya, ndipo samutama Mulungu mopemba. Tsonotu iwo adzachita mantha aakulu, mantha ake amene sadaoneke ndi kale lonse. Pakuti Mulungu adzaononga adani okuzingani. Inu mudzaŵachititsa manyazi chifukwa Mulungu waŵakana. Chibwere ndithu chipulumutso cha Israele kuchokera ku Ziyoni! Mulungu akadzaŵabwezera ufulu anthu ake, Yakobe adzakondwera, Israele adzasangalala kwambiri. Inu Mulungu, pulumutseni ndi dzina lanu, onetsani ndi mphamvu zanu kuti ndine wosalakwa. Inu Mulungu, imvani pemphero langa, tcherani khutu kuti mumve mau a pakamwa panga. Anthu onyada andiwukira, anthu ankhalwe amafunafuna moyo wanga, iwo saganizako za Inu Mulungu. Komatu, Mulungu ndiye amandithandiza, Ambuye ndiwo amachirikiza moyo wanga. Adzaŵabwezera adani anga zoipa. Aonongeni, Inu Ambuye, chifukwa cha kukhulupirika kwanu. Ndidzapereka nsembe kwa Inu mwaufulu. Ndidzatamanda dzina lanu, Inu Chauta, popeza kuti ndinu abwino. Mwandipulumutsa m'mavuto anga onse, ndakondwa poona adani anga atagonja. Inu Mulungu, tcherani khutu kuti mumve pemphero langa, musabisale pamene ndikukupembani. Mundimvere, ndipo mundiyankhe. Mtima wanga suli m'malo chifukwa cha mavuto anga. Ndikuda nkhaŵa chifukwa adani anga akundifuulira, anthu oipa akundipsinja. Akundivutitsa kwambiri, akundikwiyira kosalekeza. Mtima wanga ukumva ululu woopsa, zoopsa za imfa zandigwera. Mantha andifikira, ndipo ndikunjenjemera, mantha aakulu andigwira. Ndipo ndimati, “Ndikadakhala ndi mapiko onga a njiŵa, bwenzi nditauluka kupita kutali kukapuma. Inde, ndikadathaŵira kutali ndi kukakhala ku chipululu. “Ndikadafulumira kupeza pobisalira mphepo yaukali yamkunthoyi.” Inu Ambuye, onongani zolinga za adani anga, musokoneze upo wao. Pakuti ndikuwona anthu akuchita chiwawa ndi nkhondo mumzindamo. Usana ndi usiku iwo akuuzungulira pa makoma ake, mumzindamo muli chiwawa ndi nkhondo. M'menemo muli chiwonongeko chokhachokha. M'misika yake muli zopanikizana ndi zonyenga. Akadakhala mdani wanga wondinyozayo, ndikadatha kupirira. Akadakhala mdani wanga wondichita chipongweyo, ndikadangobisala basi. Koma iweyo mnzanga, mnzanga woyenda naye, bwenzi langa wozoloŵerana naye, ndi amene ukuchita zimenezi. Tinkakambirana nkhani zokoma tili aŵiri, tinkapembedza limodzi m'Nyumba ya Mulungu. Inu Mulungu, mulole kuti imfa iŵagwere adani anga, atsikire ku manda akadali moyo, pakuti zoipa zili tho m'mitima ndi m'nyumba zao. Koma ine ndikupempha Chauta, ndipo Iye adzandithandiza. Madzulo, m'maŵa ndi masana ndikudandaula ndi kulira, ndipo Iye adzamva mau anga. Adzapulumutsa moyo wanga pa nkhondo imene ndikumenya, pakuti anthu ambiri akukangana nane. Mulungu, amene akukhala pa mpando waufumu kuyambira kalekale, adzandimenyera nkhondo, adzaŵatsitsa adani anga chifukwa safuna kusintha khalidwe lao loipa, ndipo saopa Iye. Mnzanga adatambasula dzanja lake kuti amenye abwenzi ake, adaphwanya chipangano chake. Mau ake anali osalala kupambana batala, komabe mumtima mwake munali zankhondo. Mau ake anali ofeŵa kupambana mafuta, komabe anali ndi malupanga osololasolola. Tula kwa Chauta nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakuchirikiza. Sadzalola konse kuti wolungama wake agwedezeke. Koma Inu Mulungu mudzaŵaponya adani anga m'dzenje lozama lachiwonongeko. Anthu okhetsa magazi ndi onyenga sadzafika ngakhale theka la masiku ao. Koma ine ndidzadalira Inu. Inu Mulungu, mundichitire chifundo, pakuti anthu akundizunza. Adani akundithira nkhondo ndi kundipsinja tsiku lonse. Adani akundizunza tsiku lonse, pali ambiri amene akumenyana nane monyada. Pamene ndichita mantha ndimadalira Inu. Ndimatamanda Mulungu chifukwa cha zimene wandilonjeza. Ndimakhulupirira Mulungu mopanda mantha. Kodi munthu angandichite chiyani? Tsiku lonse adaniwo amafunafuna kulepheretsa zolinga zanga. Zonse zimene amaganiza ndi zoti andichite zoipa. Amasonkhana okhaokha namabisalira, amalonda mayendedwe anga, amafuna kundipha. Muŵalange chifukwa cha zoipa zao. Inu Mulungu, muŵakwiyire anthuwo ndi kuŵaononga. Inu mwaona kupiripita kwanga, mudziŵa kuchuluka kwa misozi yanga. Kodi zonsezi sizidalembedwe m'buku lanu? Tsono adani anga adzabwezedwa m'mbuyo pa tsiku lomwe ndidzaitana Mulungu. Ndikudziŵa kuti Mulungu ali pa mbali yanga. Ndimatamanda Mulungu chifukwa cha mau ake. Ndimatamanda Chauta chifukwa cha zimene wandilonjeza. Ndimadalira Mulungu, sindidzachita mantha konse. Kodi munthu angandichite chiyani? Ndiyenera kuchita zimene ndidalumbira kwa Inu Mulungu. Ndidzapereka kwa Inu nsembe zothokozera. Pakuti mwalanditsa moyo wanga ku imfa. Inde mwandichirikiza mapazi kuti ndisagwe, kuti motero ndiziyenda pamaso pa Mulungu m'kuŵala kwa amoyo. Mundichitire chifundo Inu Mulungu, mundichitire chifundo, pakuti mtima wanga ukudalira Inu. Ndidzathaŵira pansi pa mapiko anu, mpaka chiwonongeko chitandipitirira. Ndikulirira Mulungu Wopambanazonse, Mulungu amene amandichitiradi zonse zimene walonjeza. Mulungu adzandiyankha ali kumwamba, ndipo adzandipulumutsa. Iye adzasokoneza amene andipondereza. Adzaonetsa chikondi chake chosasinthika, adzaonetsa kukhulupirika kwake. Ndimagona pakati pa anthu olusa amene ali ngati mikango. Mano ao ali ngati mikondo ndi mivi, lilime lao lili ngati lupanga lakuthwa. Inu Mulungu, onetsani ukulu wanu kumwambamwamba, wanditsani ulemerero wanu pa dziko lonse lapansi. Iwo aja adatchera mapazi anga ukonde. Mtima wanga umavutika kwambiri. Akumba mbuna m'njira yanga, koma agweramo okha. Inu Mulungu, mtima wanga wakonzeka, ndithu mtima wanga wakonzekadi. Ndidzaimba nyimbo, nyimbo yake yotamanda. Lumpha iwe mtima wanga. Inu zeze ndi pangwe, tiyeni lirani, Ndidzadzutsa dzuŵa ndi nyimbo zanga. Ndidzakuthokozani, Inu Chauta, pakati pa mitundu ya anthu. Ndidzaimba nyimbo zokutamandani pakati pa anthu a maiko onse, pakuti chikondi chanu chosasinthika nchachikulu, chofika mpaka mlengalenga, kukhulupirika kwanu kumafika mpaka ku mitambo. Inu Mulungu, onetsani ukulu wanu mumlengalenga monse. Wanditsani ulemerero wanu pa dziko lonse lapansi. Kodi mumagamuladi molungama, inu akuluakulu oweruza? Kodi mumaweruzadi anthu mwachilungamo? Iyai, mitima yanu imangolingalira zoipa, kuweruza kwanu kosalungama kumadzetsa chiwawa. Anthu oipa ndi osokera kuyambira ali m'mimba mwa mai ao, anthu amabodza ndi otayika kuyambira tsiku la kubadwa kwao. Ali ndi ululu wonga wa njoka, ali ngati mphiri yogontha, imene yatseka makutu ake, kotero kuti siimva liwu loitana la kamatsenga, ngakhale akhale wochenjera chotani. Inu Mulungu, gululani mano a m'kamwa mwao, phwanyani nsagwada za mikangoyi, Inu Chauta. Azimirire ngati madzi opita, mivi yao iŵafotere m'manja ngati udzu. Akhale ngati nkhonodambe imene imazimirira poyenda, ngati mtayo wosaona dzuŵa. Miphika yanu isanagwire moto wa nkhuni zaminga, zingakhale zaziŵisi kapena zoyaka, Mulungu aziseseretu nkuzichotsa. Munthu wangwiro adzakondwera poona kulipsirako. Adzasamba mapazi ake m'magazi a anthu oipawo. Motero anthu adzati, “Zoona, olungama amalandiradi mphotho. Alipodi Mulungu amene amaweruza pa dziko lapansi.” Pulumutseni kwa adani anga, Inu Mulungu wanga, tetezeni kwa anthu ondiwukira. Pulumutseni kwa anthu ochita zoipa, landitseni kwa anthu okhetsa magazi. Onani, iwo akubisalira moyo wanga, anthu oopsa agwirizana kuti andithire nkhondo. Ngakhale sindidachite choipa kapena kuchimwa konse, Inu Chauta, ngakhale sindidalakwe, anthuwo akuthamanga kukonzekera nkhondo. Dzambatukani, mudzandithandize, ndipo muwone. Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, ndinu Mulungu wa Israele. Dzambatukani kuti mulange anthu onse akunja. Musasiye ndi mmodzi yemwe mwa anthu onyengawo, ochita chiwembu. Amabweranso madzulo aliwonse akuuwa ngati agalu, nkumangoyendayenda mu mzinda. Awo ali ukowo, akulongolola kwambiri, ndipo akufuula mwankhalwe, chifukwa m'maganizo mwao amati, “Ndani akutimva nanga?” Koma Inu Chauta, mumangoŵaseka. Inu mumanyozera anthu onse akunja. Inu mphamvu zanga, maso anga ali pa Inu, pakuti Inu Mulungu ndinu linga langa. Mulungu wanga adzandichingamira chifukwa ndi wa chikondi chosasinthika. Mulungu wanga adzandilola kuti ndisangalale poona adani anga atagonja. Musaŵaphe pomwepa, kuwopa kuti anthu anga angaiŵale, koma muŵabalalitse ndi mphamvu zanu, ndipo muŵagwetse, Inu Ambuye, Inu chishango changa. Akodwe ndi kunyada kwao, chifukwa cha uchimo wa m'kamwa mwao, ndi mau a pakamwa pao. Chifukwa chakuti amatemberera ndipo amanama, muŵakwiyire ndi kuŵaononga. Muŵaonongeretu kuti asakhaleponso, anthu azidziŵa kuti Mulungu ndiye wolamulira Yakobe, mpaka ku mathero a dziko lapansi. Amabweranso madzulo aliwonse akuuwa ngati agalu, nkumangoyendayenda mu mzinda. Amanka nafunafuna chakudya ndipo amangofuula akapanda kukhuta. Koma ndidzaimba nyimbo zotamanda mphamvu zanu, m'maŵa ndidzaimba mokweza nyimbo zoyamika chikondi chanu chosasinthika. Pakuti Inu mwakhala ngati linga langa ndi malo othaŵiramo pa nthaŵi ya mavuto anga. Inu mphamvu zanga, ndidzakuimbirani nyimbo zokuyamikani, pakuti Inu Mulungu ndinu linga langa, ndinu Mulungu wondiwonetsa chikondi chosasinthika. Inu Mulungu mwatitaya ife, mwatiwonongera otiteteza. Mwatikwiyira, tibwezeni mwakale. Inu mwagwedeza dziko ndi chivomezi, Inu mwaling'amba. Konzani ming'alu yake, pakuti likugwedezeka koopsa, Inu mwalola anthu anu kuti aone mavuto aakulu. Mwatipatsa vinyo wachilango kuti timwe, ndipo tikudzandira naye. Komabe Inu mwatikwezera mbendera ife amene timakuwopani, kuti tisonkhanireko pothaŵa uta wankhondo. Tipambanitseni pa nkhondo ndi dzanja lanu lamanja, mutiyankhe kuti ife, okondedwa anu, tipulumuke. Mulungu ali ku malo ake oyera, walonjeza kuti, “Ndidzakugaŵirani dziko la Sekemu mokondwa, ndidzakulemberani malire m'chigwa cha Sukoti. “Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanga. Efuremu ali ngati chisoti changa chodzitetezera, Yuda ali ngati ndodo yanga yaufumu. “Mowabu adzakhala ngati mbale yosambiramo ine. Edomu adzakhala poponda nsapato zanga. Ndidzafuula mokondwa nditagonjetsa Filistiya.” Ndani adzandifikitse ku mzinda wamalinga? Ndani adzanditsogolere ku Edomu? Si wina ai koma ndinu Mulungu amene mwatitaya, ndinu Mulungu amene mwaleka kuperekeza ankhondo athu. Tithandizeni kulimbana ndi adani athuwo, pakuti chithandizo cha munthu nchopandapake. Mulungu akakhala nafe, tidzamenya nkhondo molimba mtima, pakuti ndiye amene adzapondereza adani athu. Inu Mulungu, imvani kulira kwanga, mverani pemphero langa. Ine wokhala ku mathero a dziko lapansi, ndataya mtima, ndipo ndikuitana Inu. Munditsogolere ku thanthwe lalitali. Inutu ndinu kothaŵira kwanga, nsanja yolimba yonditeteza kwa adani. Mundilole ndizikhala m'Nyumba mwanu nthaŵi zonse. Mundilole ndibisale pansi pa mapiko anu kuti munditeteze. Inu Mulungu, mwamva zimene ndalumbira popemphera. Inu mwandipatsa choloŵa chimene amalandira anthu oopa dzina lanu. Talikitsani moyo wa mfumu, zaka zake zifikire ku mibadwo ndi mibadwo. Akhale pa mpando wake waufumu pamaso pa Mulungu mpaka muyaya. Inu Chauta, mumsunge mokhulupirika chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika. Motero nthaŵi zonse ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu, tsiku ndi tsiku ndidzachitadi zimene ndidalumbirazo. Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chipulumutso changa chimafumira kwa Iye. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa, chipulumutso changa, ndi linga langa. Sindidzagwedezeka konse. Kodi nonsenu mudzaukira munthu mpaka liti, kuti mumgwetse pansi ngati khoma lopendekeka, ngati mpanda wogwedezeka? Cholinga chao nchongofuna kumtsitsa pa malo ake aulemu. Amakonda kulankhula zonama. Amadalitsa ndi pakamwa pao, koma mumtima mwao amatemberera. Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chikhulupiriro changa nchofumira kwa Iye. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, ndiye linga langa ndipo sindidzagwedezeka. Chipulumutso changa ndi ulemerero wanga, zonsezo zili kwa Mulungu. Mulungu ndiye thanthwe langa lamphamvu, ndiye kothaŵira kwanga. Anthu inu, ikani mtima wanu pa Iye nthaŵi zonse. Muuzeni zonse za kukhosi kwanu. Mulungu ndiye kothaŵira kwathu. Anthu otsika ndi mpweya chabe, ngakhale anthu okwera ndi nthunzi chabe, onsewo ndi oluluka pa sikelo, ndi opepuka kupambana mpweya. Musakhulupirire kuti zachiwawa zingakuthandizeni. Musaganize kuti kuba kungakupindulitseni. Chuma chikachuluka musaikepo mtima. Mulungu adalankhula kamodzi, ine ndaphunzirapo zinthu ziŵiri, china ndi chakuti mphamvu ndi zanu, Inu Mulungu, chikondi chanu nchosasinthika, Inu Ambuye; china ndi chakuti Inu mumabwezera munthu molingana ndi ntchito zake. Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ndimakufunafunani. Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka Inu ngati dziko louma, loguga ndi lopanda madzi. Ndikukhumbira kukuwonani m'malo anu oyera ndi kuwona mphamvu zanu ndi ulemerero wanu. Ndidzakutamandani chifukwa chikondi chanu nchabwino kupambana moyo. Choncho ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga. Ndidzakweza manja anga kwa Inu mopemphera. Mudzandikhutitsa ndi zonona, ndipo ndidzakutamandani ndi mau osangalala. Ndikagona pabedi panga ndimalingalira za Inu, usiku wonse ndimasinkhasinkha za Inu. Inu mwakhala chithandizo changa, motero ndikuimba ndi chimwemwe pansi pa mapiko anu. Mtima wanga ukukangamira Inu, dzanja lanu lamanja likundichirikiza. Koma anthu amene amayesayesa kuwononga moyo wanga, adzatsikira ku dziko la anthu akufa. Iwo adzaperekedwa kuti akaphedwe ku nkhondo, motero adzasanduka chakudya cha nkhandwe. Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu. Onse olumbirira Iye, adzamtamanda, koma pakamwa pa anthu abodza padzatsekedwa. Imvani mau anga, Inu Mulungu, pamene ndikukudandaulirani. Tetezani moyo wanga kwa mdani woopsa. Tchinjirizeni ku upo wachiwembu wa anthu oipa, tetezeni ku chiwawa cha anthu ochita zoipa. Iwo amanola lilime lao ngati lupanga, amaponya mau obaya ngati mivi. Amabisalira anthu osalakwa namaŵalasa modzidzimutsa ndi mopanda mantha. Amalimbikira za chiwembu chao, amakambirana zoti atche misampha yobisika, amanena kuti, “Angatiwone ndani?” Amaganizira zoipa nkumati, “Takonza mochenjera ndithu chiwembu chathu.” Malingaliro ndi zofuna za mtima wa munthu nzobisika. Koma Mulungu adzaŵaponya mivi. Motero mwadzidzidzi iwo adzalasidwa. Adzaŵaononga chifukwa cha zokamba zao, onse oŵapenya adzapukusa mitu. Pompo anthu onse adzachita mantha, adzasimba zimene Mulungu wachita, adzalingalira zomwe Mulungu wachitazo. Chauta adalitse anthu ake mtendere ndi chimwemwe zikhale nao, anthu akondwere chifukwa cha Chauta Inu Mulungu, anthu azikutamandani ku Ziyoni, achitedi zimene adalumbira kwa Inu. Inu amene mumamvera pemphero, anthu onse adzabwera kwa Inu, chifukwa cha machimo ao. Pamene zochimwa zathu zitipambana, Inu mumazifafaniza. Ngwodala munthu amene Inu mumamsankha nkubwera naye kudzakhala m'mabwalo anu. Mutikhutitse ndi zinthu zabwino za m'Nyumba yanu, Nyumba yanu yoyera. Tsono Inu mumatiyankha potipulumutsa ndi ntchito zanu zodabwitsa, Inu Mulungu Mpulumutsi wathu. Anthu a pa dziko lonse lapansi ndiponso a patsidya pa nyanja zakutali, onsewo amakhulupirira Inu. Inu mudaonetsa mphamvu zanu, pokhazikitsa mapiri. Inu mumachititsa bata mkokomo wa nyanja ndi mkokomo wa mafunde ndi phokoso la mitundu ina ya anthu. Motero okhala ku malire akutali a dziko lapansi amaopa zizindikiro zanu zodabwitsa. Anthu amafuula mokondwera chifukwa cha zochita zanu, kuyambira mbali imodzi ya dziko lapansi mpaka mbali yake inanso. Tsono Inu mumadalitsa dziko lapansi ndi kulithirira, ndipo mumalilemeza kwambiri. Mtsinje wa Mulungu ndi wodzaza ndi madzi, Inu mumaŵapatsa anthu dzinthu, pakuti ndimo m'mene mwalikonzera dzikolo. Inu mumathirira kwambiri makwaŵa am'mizere, mumasalaza nthumbira zake, mumafeŵetsa nthaka ndi mvula, ndipo mumadalitsa mbeu. Pakutha pa chaka mumapereka zokolola zambiri mwa ubwino wanu, kulikonse kumene Inu mupita, kumapezeka dzinthu dzambiri. Ngakhale ku mabusa akuchipululu kumamera msipu wambiri, ndipo mapiri amadzazidwa ndi chimwemwe. Madambo adzaza ndi zoŵeta, zidikha zadzaza ndi dzinthu, zonsezo zikufuula ndi kuimbira limodzi mwachimwemwe. Tamandani Mulungu ndi chimwemwe mokweza mau, inu anthu onse a pa dziko lapansi. Imbani nyimbo zoyamika dzina lake laulemerero, mumtamande mwaulemu. Muuzeni Mulungu kuti, “Ntchito zanu nzodabwitsa kwambiri. Mphamvu zanu nzazikulu, kotero kuti adani anu amakuŵeramirani moopa. Anthu onse a pa dziko lapansi amakupembedzani, amaimba nyimbo zotamanda Inu, amaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.” Bwerani mudzaone zimene Mulungu wachita, ntchito zake nzodabwitsa pakati pa anthu. Adasandutsa nyanja kuti ikhale nthaka youma. Anthu adaoloka mtsinje uja poyenda pansi. Nchifukwa chake timukondwerere Iye. Iye amalamula ndi mphamvu zake mpaka muyaya, maso ake amalonda mitundu ina ya anthu. Anthu oukira asadzikweze. Lemekezani Mulungu wathu, inu mitundu ya anthunu, mau omtamanda Iye amveke. Iye watchinjiriza moyo wathu, sadalole kuti mapazi athu aterereke. Inu Mulungu, mwatiyesa, mwatiyeretsa monga m'mene amayeretsera siliva. Inu mudatiloŵetsa mu ukonde wa adani, mudatisenzetsa katundu wolemera pamsana pathu. Inu mudalola kuti adani atikwere pa mutu, tidaloŵa m'moto ndiponso m'madzi, komabe Inu mwatifikitsa ku malo opulumukirako. Ndidzabwera ku Nyumba yanu ndi nsembe zopsereza, ndidzachitadi zimene ndidazilumbira kwa Inu, zimene ndidalankhula ndi pakamwa panga, ndiponso zimene ndidalonjeza pamene ndinali pa mavuto. Ndidzapereka kwa Inu nsembe zopsereza za nyama zonenepa, utsi wa nsembe za nkhosa zamphongo udzafika kwa Inu. Ndidzaperekanso ngati nsembe ng'ombe zamphongo ndi mbuzi. Bwerani mudzamve, inu nonse amene opembedza Mulungu, ndidzakusimbireni zimene Iye wandichitira. Ndidafuula kwa Iye, ndipo ndidamtamanda ndi pakamwa panga. Ndikadazindikira choipa chilichonse mumtima mwanga ndi kuchibisa, Ambuye sakadandimvera. Koma zoonadi, Mulungu wandimvera, wasamala mau a pemphero langa. Mulungu atamandike chifukwa sadakane pemphero langa, sadachotse chikondi chake chosasinthika kwa Ine. Inu Mulungu mutikomere mtima ndi kutidalitsa, mutiwunikire ndi chikondi chanu, Njira yanu idziŵike pa dziko lonse lapansi, chipulumutso chanu chidziŵike pakati pa mitundu yonse. Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu, mitundu yonse ya anthu ikuyamikeni. Mitundu ya anthu isangalale ndi kuimba ndi chimwemwe, chifukwa Inu mumaweruza anthu mwachilungamo, ndi kuŵatsogolera pa dziko lapansi. Mitundu yonse ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu, mitundu yonse ya anthu ikuyamikeni. Nthaka yabereka zipatso zake, Mulungu, Mulungu wathu watidalitsa. Inde, Mulungu watidalitsa, anthu onse a ku mathero a dziko lapansi apembedze Iye. Mulungu adzambatuke, adani ake amwazikane. Onse amene amamuda, athaŵe pamaso pake. Amwazeni iwowo monga m'mene mphepo imachitira utsi. Anthu oipa aonongeke pamaso pa Mulungu, monga m'mene sera amasungunukira pa moto. Koma anthu anu Mulungu, akondwere, asangalale pamaso panu, inde, asekere ndi chimwemwe. Muimbireni Mulungu, imbani nyimbo zotamanda dzina lake. Kwezani nyimbo yotamanda Iye amene amayenda pa mitambo. Dzina lake ndi Chauta, musangalale pamaso pake. Atate a ana amasiye ndiponso mtetezi wa azimai amasiye, ndi Mulungu amene amakhala m'malo ake oyera. Anthu osiyidwa, Mulungu amaŵapatsa malo okhalamo, am'ndende amaŵatulutsa kuti akhale pa ufulu, koma anthu oukira, amaŵapirikitsira ku nthaka yoguga. Inu Mulungu, pamene munkatsogolera anthu anu, pamene munkayenda m'chipululu muja, dziko lidagwedezeka, mlengalenga udagwetsa mvula chifukwa cha kubwera kwanu, Inu Mulungu. Phiri la Sinai lidagwedezeka chifukwa cha kubwera kwanu, Inu Mulungu, Mulungu wa Israele. Inu Mulungu, mudagwetsa mvula yokwanira pa dziko. Mudalimbitsanso dziko, choloŵa cha anthu anu, pamene lidaali lofooka. Anthu anu adapezamo malo okhala. Inu Mulungu, mudapatsa anthu osauka zosoŵa zao mwa ubwino wanu. Ambuye apereka lamulo. Nchachikulu chiŵerengero cha amene abwera ndi uthenga wakuti, “Mafumu a magulu a ankhondo akuthaŵa, indedi akuthaŵa. Tsono azimai ku mudzi akugaŵana zofunkha, ngakhale atsalira pakati pa makola ankhosa. “Zofunkhazo zikuwoneka ngati mapiko a nkhunda okutidwa ndi siliva, nthenga zake nzokutidwa ndi golide wonyezemira.” Pamene Mphambe adabalalitsa mafumu kumeneko, ku Zalimoni kudagwa chisanu choopsa. Iwe phiri la Basani, phiri laulemerero, Iwe phiri la Basani, phiri la nsonga zambiri! Iwe phiri la nsonga zambiriwe, chifukwa chiyani ukuliyang'ana mwansanje phiri limene Mulungu adasankha kuti azikhalapo? Ndithu Chauta adzakhalapo mpaka muyaya. Ambuye adafika ku malo ao oyera kuchokera ku Sinai, ali ndi magaleta amphamvu zikwi zambirimbiri. Inu mudakwera kumwamba, mutatenga am'ndende ambiri, ndipo mudalandira mphatso kwa anthu, ngakhale kwa anthu oukira, kuti mudzakhale kumeneko, Inu Chauta Mulungu. Atamandike Ambuye, Mulungu Mpulumutsi wathu, amene amanyamula katundu wathu tsiku ndi tsiku. Mulungu wathu ndi Mulungu wotilanditsa, ndi Mulungu, Ambuye amene amatipulumutsa ku imfa. Koma Mulungu adzatswanya mitu ya adani ake, mitu ya anthu onse oyenda m'machimo ao. Ambuye adati, “Ndidzaŵabweza adani anu kuchokera ku Basani, ndidzaŵabweza kuchokera ku nyanja yozama, kuti musambe mapazi anu m'magazi, kuti agalu anu anyambiteko magazi a adaniwo.” Inu Mulungu, mdipiti wa anthu anu oyenda mwaulemu ukuwoneka, mdipiti wolemekeza Mulungu wanga, Mfumu yanga, wokaloŵa m'malo opatulika. Oimba nyimbo zapakamwa atatsogola, oimba ndi zipangizo ali pambuyo, anamwali oimba ting'oma ali pakati. “Tamandani Mulungu mu msonkhano waukulu. Tamandani Chauta, inu zidzukulu za Israele.” Patsogolo pao pali Benjamini mng'ono wa onsewo, akalonga a Yuda ali pambuyo, ndiponso akalonga a Zebuloni ndi akalonga a Nafutali. Kungani mphamvu zanu, Inu Mulungu, onetsani mphamvu zanu, Inu Mulungu, amene mumatichitira zamphamvu. Chifukwa cha Nyumba yanu ya ku Yerusalemu, mafumu amabwera ndi mphatso kwa Inu. Dzudzulani zilombo zija zokhala m'mabango, ndiponso gulu la nkhunzi lija ndi malikonyani, ndiye kuti akalonga ndi anthu ao. Ponderezani amene amalakalaka ndalama moipa. Abalalitseni anthu okonda nkhondo. Akazembe adzabwera kuchokera ku Ejipito. A ku Etiopiya adzafulumira kugonjera Mulungu pokweza manja ao kwa Iye. Imbirani Mulungu nyimbo, inu maufumu a pa dziko lapansi. Imbani nyimbo zotamanda Ambuye, Chauta amene amayenda mu mlengalenga, mlengalenga wakalekale. Imvani liwu lake, liwu lake lamphamvu zedi. Vomerezani kuti Mulungu ndi wamphamvu, ulamuliro wake uli pa Israele, mphamvu zake zili mu mlengalenga. Mulungu ndi woopsa m'malo ake opatulika, Mulungu wa Israele ndiye amapatsa mphamvu ndi kuŵalimbikitsa anthu ake. Mulungu atamandike. Inu Mulungu, pulumutseni, pakuti madzi ayesa m'khosi. Ndamira m'thope lozama m'mene mulibe popondapo polimba. Ndaloŵa m'madzi ozama, ndipo mafunde andimiza. Ndafooka ndi kulira kwanga, kum'mero kwanga kwauma. M'maso mwada pamene ndikuyembekezera Mulungu wanga. Anthu odana nane popanda chifukwa ndi ochuluka kupambana tsitsi la kumutu kwanga. Ndi amphamvu anthu ongofuna kundiwononga, ndi kundineneza ndi mabodza ao. Kodi ndiyenera kubweza zimene sindinabe? Inu Mulungu, mumadziŵa kupusa kwanga, zolakwa zanga sizili zobisika pamaso panu. Inu Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, musalole kuti ndiŵachititse manyazi anthu okhulupirira Inu. Inu Mulungu wa Israele, musalole kuti anthu okufunafunani anyozeke chifukwa cha ine. Pakuti ndanyozedwa, nkhope yanga yagwidwa ndi manyazi chifukwa cha Inu. Kwa abale anga ndasanduka mlendo, kwa ana a mai wanga ndili ngati wakudza. Changu chochitira Nyumba yanu chandiphetsa, chipongwe cha anthu okunyozani chandigwera. Pamene ndidadzilanga posala zakudya, anthu adandinyoza. Pamene ndidavala chiguduli kuwonetsa chisoni, ndidasanduka chinthu choŵaseketsa. Anthu okhala pa chipata amandinena, ndipo zidakwa zimandiimba nyimbo. Koma ine ndimapemphera kwa Inu Chauta. Mundiyankhe pa nthaŵi yabwino, Inu Mulungu, chifukwa cha kukula kwa chikondi chanu chosasinthika, ndi chithandizo chanu chokhulupirika. Pulumutseni kuti ndisamire m'matope, landitseni kwa adani anga ndi ku madzi ozama. Musalole kuti chigumula chindikokolole, kapena kuti nyanja yakuya indimize. Musalole kuti manda atseke kukamwa atandimeza. Mundiyankhe, Inu Chauta, pakuti chikondi chanu chosasinthika nchabwino. Munditchere khutu chifukwa cha chifundo chanu chachikulu. Musandibisire ine mtumiki wanu nkhope yanu, fulumirani kundithandiza, pakuti ndili pa zovuta. Senderani pafupi, mundiwombole, mundipulumutse kwa adani anga. Inu mumadziŵa m'mene anthu amandinyozera, m'mene amandichititsira manyazi ndi kundichotsera ulemu. Adani anga onse mumaŵadziŵa. Mtima wanga wasweka chifukwa cha zipongwe, ndataya mtima kotheratu. Ndidafunafuna ena ondichitira chifundo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe. Ndidafunafunanso ena ondisangalatsa, koma sindidampeze ndi mmodzi yemwe. Adandipatsa ulembe kuti ndidye, ndipo nditamva ludzu, adandipatsa vinyo wosasa kuti ndimwe. Zakudya zao zisanduke msampha. Akodwe ndi maphwando a nsembe zao. Maso ao achite chidima kuti asathe kupenya, ziwuno zao zizinjenjemera kosalekeza. Muŵagwetsere ukali wanu, mkwiyo wanu woyaka moto uŵagwire. Zithando zao zisanduke zopanda anthu, m'mahema mwao musatsale munthu ndi mmodzi yemwe. Iwo amazunza amene Inu mwamkantha, ndipo amene Inu mwamupweteka, iwo amaonjezera kumuvutitsa. Muŵalange pa cholakwa chao chilichonse, musagamule kuti alibe mlandu. Muŵafafanize m'buku la amoyo, asalembedwe pamodzi ndi anthu anu. Koma ine ndazunzika ndipo ndikumva kuŵaŵa. Nyamuleni Inu Mulungu, kuti ndipulumuke. Ndidzatamanda dzina la Mulungu pomuimbira nyimbo, ndidzalalika ukulu wake pomuthokoza. Zimenezi zidzakondwetsa Chauta kupambana nsembe, ngakhale nsembe ya ng'ombe yamphongo. Ozunzika aone zimenezo ndipo asangalale, inu amene mumafunafuna Mulungu, mulimbenso mtima. Paja Chauta amamvera anthu osoŵa, sanyoza anthu ake omangidwa ndi unyolo. Kumwamba ndi pansi pano, nyanja ndi zonse zoyenda m'menemo zitamande Iye. Mulungu adzapulumutsa Ziyoni, ndipo adzamanganso mizinda ya Yuda. Anthu ake adzakhala kumeneko, ndipo lidzakhala dziko lao. Ana a atumiki ake nawonso adzalilandira kuti likhale lao, ndipo okonda Mulungu adzakhala m'menemo. Inu Mulungu, pulumutseni. Inu Chauta, fulumirani kudzandithandiza. Anthu ofunafuna moyo wanga, muŵachititse manyazi ndi kuŵasokoneza. Amene akhumba kundipweteka, abwezedwe m'mbuyo ndi kunyozedwa. Amene amandinyodola kuti, “Ha, Ha,” achoke ndi manyazi poona kuti alephera. Koma onse okufunafunani akondwe ndi kusangalala chifukwa cha Inu. Onse okondwerera chipulumutso chanu, azinena kosalekeza kuti, “Chauta ndi wamkulu.” Inu Chauta, ine ndine wolefuka ndi wosoŵa, bwerani msanga kwa ine, Inu Mulungu. Inu ndinu mthandizi wanga ndi Mpulumutsi wanga. Inu Mulungu wanga, musachedwe kudzandithandiza. Ine ndimathaŵira kwa Inu Chauta. Musandichititse manyazi. Koma mundilanditse ndi kundipulumutsa, pakuti ndinu Mulungu wolungama. Tcherani khutu kuti mundimve, ndipo mundipulumutse. Mundikhalire thanthwe lothaŵirako, ndiponso linga lolimba lopulumukirako. Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa. Landitseni Inu Mulungu wanga kwa anthu oipa, landitseni ku mphamvu za anthu osalungama ndi ankhalwe. Inu Ambuye, ndinu amene ndimakukhulupirirani, Inu Chauta, ndinu amene ndimakudalirani kuyambira ubwana wanga. Inu mwakhala wondichirikiza kuyambira pa nthaŵi imene ndidabadwa. Inu ndinu amene mudanditulutsa m'mimba mwa mai wanga. Ndimatamanda Inu nthaŵi zonse. Ndakhala chinthu chodabwitsa kwa anthu ambiri, koma Inu ndinu wonditchinjiriza wamphamvu. Pakamwa panga pakutamanda Inu, pakulalika ulemerero wanu tsiku lonse. Musanditaye nthaŵi ya ukalamba wanga, musandisiye ndekha pamene mphamvu zanga zatha, Adani anga amandinena, anthu olondalonda moyo wanga amapangana limodzi, namanena kuti, “Mulungu wamsiya yekha. Mlondoleni, mumgwire, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe woti ampulumutse.” Inu Mulungu, musandikhalire kutali. Inu Mulungu wanga, fulumirani kudzandithandiza. Anthu ondineneza achite manyazi ndipo aonongeke. Anthu ofunafuna kundipweteka anyozedwe, ndipo achite manyazi kotheratu. Koma ine ndidzakhulupirira Inu nthaŵi zonse, ndipo ndidzapitirizabe kukutamandani. Pakamwa panga padzalankhula tsiku lonse za ntchito zanu zolungama ndi za chipulumutso chanu, popeza kuti sindidziŵa chiŵerengero chake. Ndidzabwera ndi uthenga wofotokoza za ntchito zamphamvu za Chauta. Ndidzatamanda chilungamo chanu chokha. Inu Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ubwana wanga, ndipo ndikulalikabe ntchito zanu zodabwitsa. Choncho Inu Mulungu, musandisiye ndekha ngakhale pamene ndakalamba ndipo imvi zili mbu, mpaka nditalalika mphamvu zanu kwa mibadwo yonse yakutsogolo. Mphamvu zanu ndi kulungama kwanu, zimafikira mpaka kumwambamwamba. Pali yani wofanafana nanu, Inu Mulungu, amene mwachita zazikulu? Mudzanditsitsimutsanso Inu amene mwandiwonetsa mavuto ambiri oŵaŵa, mudzanditulutsanso m'dzenje lozama la pansi pa nthaka. Inu mudzaonjezera ulemu wanga ndipo mudzandisangalatsanso. Ndidzakutamandaninso ndi zeze, Inu Mulungu wanga, chifukwa cha kukhulupirika kwanu. Ndidzaimba nyimbo zoyamika Inu ndi pangwe, Inu Woyera wa Israele. Pakamwa panga padzafuula ndi chimwemwe, pamene ndikukuimbirani nyimbo zotamanda. Nawonso mtima wanga umene mwauwombola, udzaimba moyamika. Tsiku lonse ndidzasimba za kulungama kwanu, pakuti amene ankafuna kundichita choipa, aŵachititsa manyazi ndipo aŵanyazitsa. Inu Mulungu, patsaniko mfumu nzeru zoweruzira, patsaniko mwana wa mfumu mtima wokonda chilungamo. Motero mfumuyo idzaweruza anthu anu molungama ndiponso anthu anu osauka mosakondera. Mapiri adzabweretsa madalitso kwa anthu, magomo adzadzetsa mphotho ya chilungamo. Mfumu idzateteza anthu osauka, idzapulumutsa anthu osoŵa, koma idzaononga anthu ozunza anzao. Idzakhala moyo pa mibadwo yonse, nthaŵi zonse pamene dzuŵa ndi mwezi zikuŵala mu mlengalenga. Idzakhala madalitso ngati mvula yogwa pa minda ngati mvula yowaza pa nthaka! Pa masiku ake chilungamo chidzakula, mtendere udzachuluka, mpaka mwezi utaleka kuŵala! Idzakhala ikulamulira kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja ina, kuchokeranso ku Mtsinje mpaka ku mathero a dziko. Amaliwongo akuchipululu adzaiŵeramira, adani ake adzadya fumbi. Mafumu a ku Tarisisi ndi akuzilumba adzaipatsa mitulo, mafumu a ku Sheba ndi a ku Seba adzabwera ndi mphatso. Mafumu onse adzaigwadira ndipo mitundu yonse ya anthu idzaitumikira. Ndithu iyo idzalanditsa anthu osoŵa amene amaiitana, idzapulumutsa anthu osauka ndiponso opanda woŵathandiza. Idzamvera chisoni anthu ofooka ndi osoŵa, ndipo idzapulumutsa moyo wa anthu aumphaŵi. Idzaombola moyo wao kwa anthu oŵapsinja ndi kwa oŵachita zankhanza, pakuti magazi ao ndi amtengowapatali pamaso pake. Ikhale ndi moyo wautali! Golide wa ku Sheba apatsidwe kwa mfumuyo. Anthu aipempherere nthaŵi zonse, aipemphere madalitso kosalekeza. M'dziko mukhale chakudya chambiri, pamwambanso pa mapiri pakhale dzinthu. Zipatso zake zichuluke ngati za ku Lebanoni, anthu ake achuluke m'mizindamo ngati udzu wakuthengo. Dzina lake lisaiŵalike konse, mbiri yake ikhalepobe monga momwe limakhalira dzuŵa. Anthu alandire madalitso chifukwa cha iyo, a mitundu yonse aitche yodala. Atamandike Chauta, Mulungu wa Israele. Iye yekha ndiye amene amachita zinthu zodabwitsa. Dzina lake laulemerero litamandike mpaka muyaya. Ulemerero wake udzaze dziko lonse lapansi. Inde momwemo. Inde momwemo. Ano ndiwo mathero a mapemphero a Davide, mwana wa Yese. Zoonadi, Mulungu ndi wabwino kwa olungama, kwa anthu oyera mtima. Koma ine ndinali pafupi kuphunthwa, mapazi anga anali pafupi kuterereka. Pakuti ndinkachita nsanje ndi anthu odzikuza, pamene ndidaona anthu oipa akulemera. Iwowo samva kupweteka konse. Matupi ao ndi onenepa ndi athanzi. Saona mavuto monga anthu ena, sazunzika ngati anzao. Nchifukwa chake amavala kunyada ngati mkanda wam'khosi. Amavala nkhanza ngati malaya. Maso ao ndi otupa ndi kunenepa. Mitima yao ndi yodzaza ndi maganizo ofuna kuchita zoipa. Amanyodola ndi kumalankhula zoipa, amadzikuza ndi kumaopseza ena kuti, “Tikupsinjani.” Pakamwa pao pamalankhula monyoza Mulungu kumwamba, ndipo lilime lao ndi losamangika pa dziko lapansi. Nchifukwa chake ngakhale anthu a Mulungu amabwera kwa iwo, ndipo amakhuta zonena zao ngati madzi akumwa. Amati, “Kodi Mulungu angadziŵe bwanji? Kodi Wopambanazonseyo angadziŵe kanthu kalikonse?” Onani, umu ndimo m'mene aliri anthu oipa. Nthaŵi zonse ali pabwino, ndipo amangolemera kosalekeza. Ine ndasunga mtima wanga woyera, ndasamba m'manja kuwonetsa kuti ndine wosalakwa, koma zonsezi popanda phindu konse. Pakuti ndapeza mavuto tsiku lonse, ndipo ndalangidwa m'maŵa mulimonse. Ndikadati, “Ndilankhula monga amachitira iwowo,” ndikadakhala wosakhulupirika kwa zidzukulu zanu, Koma pamene ndidalingalira zimenezi kuti ndizimvetse bwino, zidandiwonekera ngati nkhani yovuta, mpaka nditakaloŵa m'malo opatulika a Mulungu, apo mpamene ndidaona mathero ake a anthuwo. Zoonadi, Inu mumapondetsa anthu oipa pa malo oterera. Mumaŵagwetsa mpaka aonongeke. Adzangoferatu ndi mantha, ndi kuwonongeka pa kamphindi kochepa. Inu Ambuye, pamene mudzadzuka mudzaŵanyoza kotheratu, monga momwe munthu amanyozera maloto atadzuka m'maŵa. Pamene paja ndinkavutika ndi maganizo, ndi kumamva cholasa mumtimamu, ndinali wopusa wosamvetsa kanthu, ndinali ngati chilombo kwa Inu. Koma chonsecho ndili ndi Inu nthaŵi zonse. Inu mumandigwira dzanja lamanja. Mumandiwongolera ndi malangizo anu, pambuyo pake mudzandilandira ku ulemerero. Nanga ndili ndi yani kumwamba kupatula Inu? Pansi pano palibe kanthu kena kamene ndimafuna, koma Inu nokha. Thupi langa ndi mtima wanga zingafooke chotani, Mulungu ndiye mphamvu za mtima wanga ndiyenso wondigaŵira madalitso mpaka muyaya. Onse amene ali kutali ndi Inu adzaonongeka, Inu mumaŵaononga amene ali osakhulupirika kwa Inu. Koma ine kukhala pafupi ndi Mulungu kumandikomera. Ndatsimikiza zoti Ambuye ndiwo kothaŵira kwanga ndipo ndidzalalika ntchito zao zonse. Inu Mulungu, chifukwa chiyani mukutitaya mpaka muyaya? Chifukwa chiyani mkwiyo wanu ukutukutirira nkhosa za busa lanu ngati moto? Kumbukirani mpingo wanu umene mudaupatula kuyambira kale, mtundu umene Inu mudauwombola kuti ukhale wanuwanu. Kumbukirani phiri la Ziyoni kumene Inu mudadzakhala. Dzayendereni mabwinja oonongeka kwathunthuŵa. Adani aononga zinthu zonse za m'Nyumba yanu. Adani anu abangula m'malo anu opatulika, adaikamo mbendera zao kusonyeza kuti agonjetsa. Adadulamo zonse, monga momwe anthu amadulira mitengo m'nkhalango. Pambuyo pake, ndi nsompho ndi nyundo, adakadzula zosemasema zonse. Nyumba yanu adaitentha, malo amene Inu mumakhalako adaŵaipitsa poŵagwetsera pansi. Mumtima mwao ankati, “Tiyeni tiŵagonjetse kotheratu.” Adatentha malo opatulika onse a Mulungu m'dzikomo. Zizindikiro zonse za fuko lathu zaonongeka, kulibenso mneneri ndi mmodzi yemwe, palibe ndi mmodzi yemwe pakati pathu amene akudziŵa nthaŵi yodzatha zimenezi. Inu Mulungu, adani athuŵa adzanyodolabe mpaka liti? Amaliwongowo adzanyozabe dzina lanu mpaka muyaya? Chifukwa chiyani mukubisa dzanja lanu lotithandiza? Bwanji dzanja lanu lamanja likungokhala pachifuwa panu? Komabe Inu Mulungu, ndinu mfumu yanga kuyambira kalekale. Ndinu amene mumagwira ntchito yopulumutsa pa dziko lonse lapansi. Mudagaŵa Nyanja Yofiira ndi mphamvu zanu. Mudaphwanya mitu ya zilombo zam'madzi. Mudatswanya mitu ya Leviyatani, chilombo cham'madzi chija, nkuitaya kuti ikhale chakudya cha zilombo zam'chipululu. Mudatumphutsa akasupe ndi mifuleni, mudaumitsa mitsinje imene siiphwa. Mudalenga usana ndi usiku. Mudaika mwezi ndi dzuŵa m'malo mwake. Mudalemba malire a dziko lapansi, mudakhazikitsa chilimwe ndi dzinja. Kumbukirani, Inu Chauta, kuti adani amakunyodolani, kuti anthu achipongwe amanyoza dzina lanu. Musati mupereke moyo wa nkhunda yanu Israele ku zilombo zakuthengo. Musaiŵale mpaka muyaya moyo wa anthu anu osauka. Kumbukirani chipangano chanu, pakuti malo obisika am'dziko asanduka mochitira zankhanza zambirimbiri. Musalole kuti anthu oponderezedwa achite manyazi. Osauka ndi osoŵa akutamandeni. Dzambatukani, Inu Mulungu, tiyeni mudziteteze pa mlandu wanuwo, kumbukirani kuti anthu amwano amakunyodolani tsiku lonse. Musalekerere chiwawa cha amaliwongo anu, phokoso la adani anu limene likungokulirakulira nthaŵi zonse. Tikukuthokozani Inu Mulungu, ndithu tikukuthokozani. Tikutchula dzina lanu mopemphera ndipo tikulalika ntchito zanu zodabwitsa. Inu mukuti, “Pa nthaŵi imene ndiisankhule, ndidzaweruza mwachilungamo. Pamene dziko lapansi likugwedezeka pamodzi ndi zonse zokhalamo, ndine amene ndimachirikiza mizati yake.” Ndimauza anthu odzitama kuti, “Musadzitame,” ndiponso anthu oipa kuti, “Musadzitukumule chifukwa cha mphamvu zanu. Musadzikuze chifukwa cha mphamvu zanu, kapena kumalankhula zamwano.” Kugamula milandu sikuchokeratu kuvuma kapena kuzambwe, ndiponso sikuchokera ku chipululu. Koma ndi Mulungu yekha amene amagamula milandu, amatsitsa wina, nakweza wina. M'manja mwa Chauta mulitu chikho cha vinyo wofanizira chilango chake, vinyo wotutuma ndi wothirako dzoŵaŵa. Adzatsanyula vinyoyo, ndipo oipa onse a pa dziko lapansi adzamwa, nadzagugudiza mpaka ndungundungu zake. Koma ine sindidzaleka kukondwera, ndidzaimba nyimbo zotamanda Mulungu wa Yakobe mpaka muyaya. Iye adzaphwanya mphamvu za anthu onse oipa, koma adzaonjezera mphamvu za anthu okhulupirira. Mulungu ndi wodziŵika m'dziko la Yuda, dzina lake ndi lolemekezeka mu Israele. Hema lake adalimanga ku Yerusalemu. Malo ake okhalamo ali kumeneko ku Ziyoni. Kumeneko adathyola mivi youluzika, zishango, malupanga ndi zida zonse zankhondo za adani ake. Inu Mulungu, mukuwonetsa ulemerero ndi mphamvu kupambana mapiri a zofunkha. Mudalanda zofunkha za anthu olimba mtima, mudaŵagonetsa tulo tofa nato, ankhondo onse sankatha kuchita kanthu ndi manja ao. Pamene mudaŵaopsa, Inu Mulungu wa Yakobe, onse okwera pa akavalo ndi akavalo ao omwe adagwa nangoti kakasi. Zoonadi, Inu ndinu woopsa. Angathe kuima pamaso panu ndani pamene mkwiyo wanu wayaka? Chiweruzo chanu mudachilengeza kumwamba, anthu a pa dziko lapansi adaopa nakhala chete, pamene Inu Mulungu mudaimirira kuti muweruze anthu, ndi kupulumutsa opsinjidwa onse a pa dziko lapansi. Zoonadi, mkwiyo wa anthu umabweretsa ulemu kwa Inu, opulumuka ku mkwiyowo mumaŵasunga pafupi ndi Inu. Lumbirani kwa Chauta, Mulungu wanu, ndipo muchitedi zimene mwalumbirazo. Onse omzungulira abwere ndi mphatso kwa Iye amene ayenera kumuwopa, ndiye amene amathetsa mphamvu akalonga ndipo amaopsa mafumu a pa dziko lapansi. Ndikulira mopemba kwa Mulungu, ndi mau okweza ndikufuula kwa Mulungu kuti andimve. Pa tsiku lamavuto ndimafunafuna Ambuye. Usiku wonse ndimakweza manja anga ndi kupemphera kosalekeza. Mtima wanga umakana kuusangalatsa. Ndikamalingalira za Mulungu, ndimangobuula mumtima. Ndikamasinkhasinkha za Iye, ndimataya mtima. Mumagwira zikope zanga kuti ndisagone tulo. Ndikuvutika kwambiri kotero kuti sindingathe kulankhula. Ndimalingalira za masiku akale, ndimakumbukira zaka zamakedzana. Ndimasinkhasinkha mumtima mwanga usiku. Ndimadzifunsa ndi kufufuzafufuza mumtima mwanga. Ndimati, “Kodi Ambuye adzandikana mpaka liti? Kodi sadzandikomeranso mtima? Kodi chikondi chao chosasinthika chija chatheratu? Kodi malonjezo ao aja atha mpaka muyaya? Kodi Mulungu waiŵala kukoma mtima kwake kuja? Kodi wakwiya ndi kuleka chifundo chake chija?” “Chondiŵaŵa ndi chakuti, Mulungu Wopambanazonse wasintha mchitidwe wake.” Komabe ndidzakumbukira ntchito zanu, Inu Chauta, inde, ndidzakumbukira zodabwitsa zanu zakalekale. Ndidzasinkhasinkha za zonse zimene mwachita, ndidzalingalira za ntchito zanu zamphamvuzo. Njira zanu, Inu Mulungu, nzoyera. Kodi alipo mulungu winanso wamkulu ngati Mulungu wathu? Inu ndinu Mulungu amene mumachita zodabwitsa, amene mwaonetsa mphamvu zanu pakati pa mitundu ya anthu. Mudaombola anthu anu ndi mkono wanu wamphamvu, ndiye kuti ana a Yakobe ndi Yosefe. Pamene madzi adakuwonani, Inu Mulungu, pamene madzi adakuwonani, adachita mantha, inde, nyanja yakuya idanjenjemera. Mitambo idachucha madzi, mumlengalenga mudachita bingu. Zing'aning'ani mbali ndi mbali. Phokoso la bingu lanu lidamveka konsekonse, mphezi zanu zidaŵalitsa dziko lonse, dziko lapansi lidanjenjemera ndi kugwedezeka. Inu mudadzera pa nyanja, njira yanu idadzera pa madzi akuya, komabe mapazi anu sadaoneke. Mudatsogolera anthu anu ngati nkhosa kudzera mwa Mose ndi Aroni. Mvetsetsani zimene ndikukuphunzitsani, inu anthu anga. Tcherani khutu, mumve mau a pakamwa panga. Ndidzakusimbirani fanizo. Ndidzalankhula nkhani zobisika zakalekale, zinthu zimene tidazimva ndi kuzidziŵa, zomwe makolo athu adatifotokozera. Sitidzabisira ana ao, koma tidzafotokozera mbadwo wakutsogolo ntchito zotamandika za Chauta, tidzaŵasimbira mphamvu zake ndi zodabwitsa zimene wakhala akuchita. Adapereka mau odzichitira umboni kwa Yakobe, adakhazikitsa malamulo ake mu Israele. Adalamula makolo athu kuti aziŵaphunzitsa ana ao malamulowo. Motero mbadwo wakutsogolo wa ana amene sanabadwebe, udzaŵadziŵa, ndipo nawonso udzafotokozera ana ake. Anawo aike chikhulupiriro chao pa Mulungu, ndipo asaiŵale ntchito za Mulungu, koma asunge malamulo ake. Asakhale ngati makolo ao, anthu oukira ndi osamvera aja, mbadwo wa anthu amene mitima yao inali yosakhazikika, amene moyo wao unali wosakhulupirika kwa Mulungu. Ngakhale Aefuremu anali ndi mauta, komabe adathaŵa pa tsiku la nkhondo, sadasunge chipangano cha Mulungu, koma adakana kutsata malamulo ake. Iwo adaiŵala zimene Mulungu adachita, ndiponso zozizwitsa zimene Iye adaŵaonetsa. Mulungu adachita zodabwitsa zake, makolo ao akuwona, m'dziko la Ejipito, ku dera la Zowani. Adagaŵa nyanja pakati, kuti iwo apitepo, ndipo adaimiritsa madzi ngati makoma. Masana ankaŵatsogolera ndi mitambo, usiku ankaŵatsogolera ndi kuŵala kwamoto. Adang'amba matanthwe am'chipululu, naŵapatsa madzi ochuluka ngati amumtsinje, kuti amwe. Adatumphutsa mifuleni m'thanthwe, nayendetsa madzi ngati mitsinje. Komabe iwo adapitiriza kumchimwira, naukira Mulungu Wopambanazonse m'chipululu muja. Iwo adayesa Mulungu m'mitima mwao, pomuumiriza kuti aŵapatse chakudya chimene ankakhumba. Adalankhula motsutsana ndi Mulungu nati, “Kodi Mulungu angathe kutipatsa chakudya m'chipululu muno? Paja adamenya thanthwe, kotero kuti madzi adatumphuka, ndipo mitsinje idadzaza. Kodi angathenso kutipatsa ife anthu ake buledi kapena kutipezera nyama?” Nchifukwa chake Chauta atamva zimenezi, adapsa mtima kwambiri, adayatsira moto Yakobe, napambana kukwiyira Israeleyo, popeza kuti sadadalire Mulungu, sadakhulupirire mphamvu zake zopulumutsa. Komabe Iye adalamula mitambo yamumlengalenga, natsekula zitseko zakumwamba. Poŵagwetsera mana kuti adye, adaŵapatsa tirigu wakumwamba. Motero anthu adadya buledi wa angelo, ndipo Mulungu adaŵatumizira chakudya chochuluka. Adakunthitsa mphepo yakuvuma mu mlengalenga, adatulutsa mphepo yakumwera ndi mphamvu zake. Adaŵagwetsera nyama yochuluka ngati fumbi, mbalame zochuluka ngati mchenga wakunyanja. Adalola kuti zigwere pakati pa zithando zao, konsekonse kumalo kumene ankakhalako. Motero adadya nakhuta kwambiri, popeza kuti adaŵapatsa zakudya zimene ankakhumba. Koma nkhuli yao isanathe, asanameze nkumeza komwe chakudya chaocho, mkwiyo wa Mulungu udaŵayakira, ndipo adapha amphamvu onse pakati pao, adapha anyamata abwinoabwino onse a mu Israele. Ngakhale zinali chomwecho, iwo adapitirirabe kuchimwa, sadakhulupirire ngakhale adaona zodabwitsa zake. Choncho Mulungu adadula masiku ao kuti azimirire ngati mpweya, adadula zaka zao kuti zithere m'zoopsa. Pamene ankapha ena, otsalira ankayamba kumufunafuna. Ankalapa namafunafuna Mulungu ndi mtima wao wonse. Adakumbukira kuti Mulungu ndi thanthwe loŵateteza, kuti Mulungu Wopambanazonse ndiye Mpulumutsi wao. Koma iwo adamthyasika ndi pakamwa pao, adamnamiza ndi lilime lao. Mtima wao sunali wokhulupirika kwa Iye. Sadasunge chipangano chake. Komabe pakuti Mulungu ngwachifundo, adaŵakhululukira machimo ao, ndipo sadaŵaononge. Kaŵirikaŵiri ankadziletsa kukwiya, sadalole kuti mkwiyo wake wonse uyake. Ankakumbukira kuti iwo anali anthu chabe, ngati mphepo yopita imene siibwereranso. Kaŵirikaŵiri ankamuukira m'chipululu, ankamumvetsa chisoni. Kaŵirikaŵiri ankamuyesa, ankamputa Woyera wa Israele. Sadakumbukire mphamvu zake kapena tsiku limene adaŵaombola kwa adani ao, pamene Iye adachita zizindikiro zamphamvu ku Ejipito, ndiponso zozizwitsa zake ku dera la ku Zowani. Paja Mulungu adasandutsa madzi a mitsinje yao kuti akhale magazi, kotero kuti Aejipito sadathe kumwa madziwo. Adaŵatumira nthenje za ntchentche zimene zidaŵazunza, ndiponso achule amene adasakaza dziko lao. Adalola kuti kapuchi adye mbeu zao ndiponso kuti dzombe lidye zonse za m'minda mwao. Adaononga mphesa zao ndi matalala ndiponso mitengo yao yankhuyu ndi chisanu. Adalola kuti ng'ombe zao zife ndi matalala ndi kuti nkhosa zao zife ndi zing'aning'ani. Adagwetsa moto wa ukali wake pa iwo: adaŵapsera mtima naŵakwiyira nkuŵagwetsera mavuto. Zimenezi zinali ngati gulu la angelo oononga. Adalola kukwiya, osadziletsa, sadaŵapulumutse ku imfa, koma adapereka moyo wao ku miliri. Adapha ana achisamba onse a Aejipito, ana oyamba a mphamvu zao, m'zithando za zidzukulu za Hamu. Tsono Mulungu adaŵatulutsa anthu ake ngati nkhosa, naŵatsogolera m'chipululu ngati zoŵeta. Adaŵatsogolera bwino lomwe kotero kuti sanalikuwopa, koma nyanja idamiza adani ao. Adaŵafikitsa ku dziko lake loyera, ku dziko lamapiri limene adaŵagonjetsera ndi dzanja lake lamphamvu. Adapirikitsa mitundu ina ya anthu, kuŵachotsa m'njira. Adagaŵagaŵa dziko la anthuwo kuti likhale la anthu ake, adakhazikitsa mafuko a Israele m'midzi ya anthuwo. Komabe Aisraele adamuputa ndi kumuukira Mulungu Wopambanazonse, sadasunge malamulo ake, koma iwo adakhala okanika ndi osakhulupirika monga makolo ao. Adapotoka ngati uta wosakhulupirika. Iwo adakwiyitsa Mulungu ndi akachisi ao opembedzerako mafano ku mapiri. Adamupsetsa mtima chifukwa cha mafano ao osemawo. Pamene Mulungu adamva zimenezi, adakwiya kwambiri, ndipo adakana Aisraele kotheratu. Adasiya malo ake a Silo kumene ankakhala, adasiya hema limene ankakhalamo pakati pa anthu, ndipo adalola adani athu kuti alande Bokosi la Chipangano chake, limene linali chizindikiro cha mphamvu zake ndi ulemerero wake. Chifukwa adakwiyira anthu ake, adalola kuti anthu akewo aphedwe pa nkhondo. Nkhondo yoyaka ngati moto idaononga anyamata ao, ndipo atsikana ao adasoŵa oŵaimbira nyimbo zaukwati. Ansembe ao omwe adaphedwa ndi lupanga, ndipo akazi ao amasiye sadaŵalole kulira maliro. Pomaliza Ambuye adachita ngati kudzuka kutulo, ngati munthu wamphamvu wofuula chifukwa choledzera. Tsono Mulungu adaŵapirikitsa adani ake, naŵachititsa manyazi anthaŵizonse. Adakana banja la Yosefe, sadasankhule fuko la Efuremu. Koma adasankhula fuko la Yuda, ndiponso phiri la Ziyoni limene amalikonda. Adamanga malo ake opatulika ngati malo ake akumwamba, okhazikika ngati dziko lapansi mpaka muyaya. Mulungu adasankhula Davide mtumiki wake, ndipo adakamtenga ku makola a nkhosa. Adamtenga kumene ankaŵeta nkhosa zimene zinali ndi ana, kuti adzakhale mbusa wa Yakobe, fuko lake, wa Israele, choloŵa chake. Davide adaŵasamala ndi mtima wolungama, naŵatsogolera ndi dzanja lake mwaluso. Inu Mulungu, anthu akunja aloŵerera m'dziko la anthu anu, aipitsa Nyumba yanu yoyera. Asandutsa Yerusalemu bwinja. Ataya mitembo ya atumiki anu kwa mbalame zamumlengalenga, kuti ikhale chakudya chake, ataya matupi a anthu anu oyera mtima kwa zilombo zakuthengo. Akhetsa magazi ao ngati madzi, ponse pozungulira Yerusalemu, ndipo palibe woti nkuika maliro ao. Ife tasanduka chinthu chonyozeka kwa anzathu, anthu a mitundu ina amatinyodola ndi kutiseka. Mpaka liti, Inu Chauta? Kodi mudzakhalabe wokwiya mpaka muyaya? Kodi nsanje yanu idzayakabe ngati moto? Gwetsani ukali wanu pa mitundu ya anthu osakudziŵani, ndiponso pa maufumu osatama dzina lanu mopemba. Pakuti ameza anthu a Yakobe, ndipo dziko lao alisandutsa bwinja. Musatilange ife chifukwa cha machimo a makolo athu. Mutichitire chifundo msanga, chifukwa tatsitsidwa kwambiri. Tithandizeni, Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, kuti dzina lanu likhale ndi ulemerero. Tipulumutseni, ndipo mutikhululukire zochimwa zathu, kuti dzina lanu lilemekezeke. Chifukwa chiyani anthu akunja akuti, “Kodi Mulungu wao ali kuti?” Mulole kuti tiwone Inu mukulipsira mitundu ina ya anthu, chifukwa chokhetsa magazi a atumiki anu. Mumve kubuula kwa anthu am'ndende, muŵasunge ndi mphamvu zanu zazikulu anthu oyenera kuphedwa. Inu Ambuye, kunyoza kuja kumene anthu a mitundu ina adakunyozani, muŵabwezere kasanunkaŵiri. Pamenepo ife anthu anu, nkhosa za pa busa lanu, tidzakuthokozani mpaka muyaya, tidzakutamandani m'mibadwo yonse. Imvani, Inu Mbusa wa Israele, Inu amene mumatsogolera anthu a Yosefe ngati gulu la nkhosa. Inu amene mumakhala pa akerubi ngati pa mpando wanu wachifumu, dziwonetseni kwa mafuko a Efuremu ndi Benjamini ndi Manase. Onetsani mphamvu zanu, ndipo mubwere kudzatipulumutsa. Inu Mulungu, tibwezereni mwakale, mutiwonetse nkhope yanu yokondwa, ndipo ife tidzapulumuka. Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, mudzakwiyira mapemphero a anthu anu mpaka liti? Mwaŵadyetsa chisoni ngati chakudya, mwaŵapatsa misozi ngati chakumwa. Mwaŵasandutsa chinthu chonyozeka kwa anzathu a mitundu ina, ndipo adani athu akakhala pamodzi, amangotiseka. Inu Mulungu Wamphamvuzonse, tibwezereni mwakale, mutiwonetse nkhope yoŵala, kuti ife tipulumuke. Mudatulutsa mpesa wanu Israele m'dziko la Ejipito. Mudapirikitsa mitundu ina ya anthu kuti muubzale mpesawo. Mudaulimira munda mpesawo, udamera mizu yozama, nudzaza m'dzikolo. Mapiri adaphimbidwa ndi mthunzi wake, mikungudza yaikulu yomwe idaphimbidwa ndi nthambi zake. Nthambizo zidafika mpaka ku nyanja yaikulu yakuzambwe, ndipo mphukira zake mpaka ku mtsinje waukulu wakuvuma. Nanga chifukwa chiyani mwagumula mpanda wake, kuti opita m'njira azithyola nawo zipatso zake? Nguluŵe zam'nkhalango zimauwononga, ndipo zonse zoyenda m'thengo zimaudya. Mutembenukirenso kwa ife, Inu Mulungu Wamphamvuzonse, muyang'ane Inu okhala kumwamba, ndipo muwone. Samalani mpesawo, mtengo woyambirira umene Inu mudaubzala ndi dzanja lanu lamanja. Adani athu autentha, augwetsa pansi. Ayang'aneni iwowo mokwiya ndi kuŵaononga. Koma ndi dzanja lanu muteteze anthu amene mudaŵasankha, anthu amene Inu nomwe mwaŵalimbikitsa kuti akutumikireni. Tsono sitidzakusiyaninso, tipatseni moyo, ndipo tidzatama dzina lanu mopemba. Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, tibwezereni mwakale. Mutiwonetse nkhope yoŵala, kuti ife tipulumuke. Kwezani mau kuimbira Mulungu amene ali mphamvu zathu. Fuulani ndi chimwemwe kwa Mulungu wa Yakobe. Yambani nyimbo, imbani ng'oma, pamodzi ndi pangwe wolira bwino ndi zeze. Imbani lipenga mwezi ukaoneka chatsopano, ukaoneka kwathunthu, pa tsiku lathu lachikondwerero. Pakuti ndilo lamulo lokhalira Israele, lochokera kwa Mulungu wa Yakobe, Adalipereka lamulolo kwa zidzukulu za Yosefe pamene zinkatuluka m'dziko la Ejipito. Ndikumva liwu limene sindidalimve ndi kale lonse, lakuti, “Ndidakutulani katundu wa pamapeŵa panu. Manja anu ndidaŵachotsera ntchito yonyamula madengu. Pamene munali m'mavuto mudandiitana, Ine nkukupulumutsani. Ndidakuyankhani ndili wobisika m'bingu. Ndidakuyesani ku madzi a Meriba aja. Imvani inu anthu anga, ndikulangizeni. Inu Aisraele, chonde mukadandimvera! “Pasadzakhale mulungu wachilendo pakati panu. Musadzapembedze mulungu wina ai. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu, amene ndidakutulutsani m'dziko la Ejipito. Yasamani kukamwa, Ine ndidzakudyetsani. “Koma anthu anga sadamvere mau anga. Israele adandinyoza. Choncho ndidaŵasiya ndi mitima yao yosamverayo, kuti atsate zimene ankafuna. “Anthu anga akadandimvera, Aisraele akadayenda m'njira zanga, bwenzi posachedwa nditagonjetsa adani ao, ndipo dzanja langa likadakantha amaliwongo ao. “Anthu amene amadana ndi Chauta, akadakhwinyata pamaso pake, ndipo tsoka lao likadakhala mpaka muyaya. Ndikadakudyetsani ndi ufa wosalala watirigu, ndipo ndikadakukhutitsani ndi uchi wam'thanthwe.” Mulungu akutsogolera msonkhano wakumwamba. Akugamula mlandu milungu ya pansi pano. Akuti, “Mudzakhalabe mukuweruza mopanda chilungamo mpaka liti? Bwanji mukupitirizabe kumakondera anthu oipa? Inu tetezani anthu ofooka ndi amasiye mwachilungamo. Weruzani molungama ozunzika ndi amphaŵi. “Landitsani ofooka ndi osoŵa. Apulumutseni kwa anthu oipa.” Iwo sadziŵa kanthu ndiponso alibe nzeru, amangoyenda m'chimbulimbuli. Maziko onse a dziko lapansi agwedezeka. Ine ndikuti, “Inu ndinu milungu, nonsenu ndinu ana a Mulungu Wopambanazonse. Komabe mudzafa ngati anthu onse, ndipo mudzagwa ngati kalonga wina aliyense.” Dzambatukani, Inu Mulungu, weruzani dziko lapansi, popeza kuti mitundu yonse ya anthu ndi yanu. Inu Mulungu, musakhalenso chete. Musangoti phee, musangoti duu, Inu Mulungu. Onani, adani anu akuchita chiwawa. Amene adana nanu akukuukirani. Akuchitira anthu anu upo wonyenga. Akuŵapangira zoipa anthu anu amene mumaŵateteza. Iwo amati, “Tiyeni tifafanize mtundu wao wonse. Dzina la Israele lisakumbukikenso.” Zoonadi, akumvana popangana chiwembu, akupangana zokuukirani, anthu okhala m'mahema a Aedomu ndi Aismaele, Amowabu ndi Ahagara, Agebala ndi Aamoni ndi Aamaleke, Afilisti pamodzi ndi nzika za ku Tiro. Aasiriya nawonso agwirizana nawo, kuti alimbikitse mphamvu za ana a Loti. Muŵachite zomwe mudaŵachita Amidiyani, Sisera ndi Yabini ku mtsinje wa Kisoni, amene adaŵaononga ku Endori, ndi kuŵasandutsa ndoŵe m'nthaka. Akalonga ao muŵachite zomwe mudachita Orebu ndi Zeebu, ndipo ana a mafumu ao onse, muŵachite zomwe mudachita Zeba ndi Zalimuna, amene adati, “Tiyeni tilande dziko la Mulungu likhale lathu.” Inu Mulungu wanga, muŵasandutse ngati fumbi louluka ndi kamvulumvulu, akhale ngati mankhusu ouluka ndi mphepo. Monga momwe moto umatenthera nkhalango, monga momwe malaŵi amayakira pa mapiri, momwemonso Inu muŵapirikitse ndi mkuntho, ndipo muŵaopseze ndi kamvulumvulu wanu. Inu Chauta, muŵachititse manyazi, kuti azifunafuna dzina lanu. Achitedi manyazi ndi mantha mpaka muyaya, ndipo afe imfa yonyozeka. Adziŵe kuti Inu nokha, amene dzina lanu ndinu Chauta, ndinu Wopambanazonse wolamulira dziko lonse lapansi. Malo amene mumakhalamo, Inu Chauta Wamphamvuzonse, ndi okoma kwambiri. Mtima wanga ukulakalaka, mpaka kukomoka, kufunitsitsa kuwona mabwalo a Chauta. Inu Mulungu wamoyo, ndikukuimbirani mwachimwemwe ndi mtima wanga wonse. Ngakhale timba amapeza malo okhalapo, nayenso namzeze amamanga chisa chake m'mene amagonekamo ana ake, pafupi ndi maguwa anu, Inu Chauta Wamphamvuzonse, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga. Ngodala anthu amene amakhala m'Nyumba mwanu, namaimba nyimbo zotamanda Inu nthaŵi zonse. Ngodala anthu amene mphamvu zao nzochokera kwa Inu, amene m'mitima mwao amafunitsitsa kudzera m'miseu yopita ku Ziyoni. Akamadutsa chigwa cha Baka chopanda madzi, amachisandutsa malo a akasupe, mvula yachizimalupsa imachidzaza ndi zithaphwi. Mphamvu zao zimanka zichulukirachulukira. Mulungu wa milungu adzaoneka m'Ziyoni. Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, imvani pemphero langa. Tcherani khutu, Inu Mulungu wa Yakobe. Inu Mulungu, ndinu chishango chathu, yang'anani nkhope ya wodzozedwa wanu. Kukhala tsiku limodzi m'mabwalo anu nkwabwino kwambiri kupambana kukhala masiku ambiri kwina kulikonse. Nkadakonda kukhala wapakhomo wa Nyumba ya Mulungu wanga kupambana kukhala m'nyumba za anthu oipa. Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama. Inu Chauta Wamphamvuzonse, ngwodala munthu woika chikhulupiriro chake pa Inu. Inu Chauta, mudakomera mtima dziko lanu, mudaŵakhazikanso pabwino a m'banja la Yakobe. Mudakhululukira machimo a anthu anu, mudafafaniza zolakwa zao zonse. Mudaleka ndithu ukali wanu woopsa, mudaletsa mkwiyo wanu woyaka moto. Mutibwezerenso mwakale, Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, ndipo mutichotsere mkwiyo wanu. Kodi mudzakhalabe mukutikwiyira mpaka muyaya? Kodi mudzapitiriza kukwiya mpaka pa mibadwo yathu yonse? Kodi simudzatipatsanso moyo, kuti ife anthu anu tikondwere mwa Inu? Tiwonetseni chikondi chanu chosasinthika, Inu Chauta, ndipo mutipulumutse. Ndimve zimene Chauta adzalankhula, chifukwa adzalankhula za mtendere kwa anthu ake, kwa anthu ake oyera mtima, ngati sabwereranso ku zopusa zao. Zoonadi, Mulungu ali wokonzekera kuti apulumutse amene amamuwopa, kuti ulemerero wake ukhale m'dziko lathu. Chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika zidzakumana. Chilungamo ndi mtendere zidzagwirizana. Anthu ake adzakhala okhulupirika pansi pano, ndipo Mulungu wakumwamba adzaŵalungamitsa. Inde, Chauta adzapereka zabwino, ndipo dziko lathu lidzabereka zokolola zambiri. Mulungu ndi wolungama chikhalire, chilungamo chake chimaongolera zochita zake zonse. Tcherani khutu, Inu Chauta, ndipo mundiyankhe, pakuti ndine wosauka ndi wosoŵa. Sungani moyo wanga, pakuti ndine womvera Inu. Pulumutseni ine mtumiki wanu amene ndimadalira Inu. Inu ndinu Mulungu wanga. Mundikomere mtima, Inu Ambuye, popeza kuti ndimalirira Inu tsiku lonse. Sangalatsani mtima wa ine mtumiki wanu, pakuti ndikupereka mtima wanga kwa Inu Ambuye. Inu Ambuye ndinu abwino, ndipo mumakhululukira anthu anu. Chikondi chanu chosasinthika ndi chachikulu kwa onse amene amakupembedzani. Tcherani khutu, Inu Chauta, kuti mumve pemphero langa. Mverani kulira kwanga kopemba. Pa tsiku lamavuto ndimakuitanani, pakuti mumayankha mapemphero anga. Pakati pa milungu palibe ndi mmodzi yemwe wolingana nanu, Inu Ambuye, palibe ntchito zolingana ndi ntchito zanu. Mitundu yonse ya anthu imene mwailenga idzabwera, idzakuŵeramirani, Inu Ambuye, ndipo idzalemekeza ukulu wanu. Pakuti Inu ndinu wamkulu, mumachita zinthu zodabwitsa, Inu nokha ndinu Mulungu. Phunzitseni njira zanu, Inu Chauta, kuti ndiziyenda m'zoona zanu. Mundipatse mtima wosagaŵikana, kuti ndiziwopa dzina lanu. Inu Ambuye, Mulungu wanga, ndikukuthokozani ndi mtima wanga wonse, ndidzalemekeza ukulu wanu mpaka muyaya. Paja chikondi chanu chosasinthika kwa ine nchachikulu, Mwandipulumutsa ku malo akuya a anthu akufa. Inu Mulungu, anthu achipongwe andiwukira. Anthu opanda chifundo akufunafuna moyo wanga ndipo sasamala za Inu. Koma Inu Ambuye, ndinu Mulungu wachifundo ndinu Mulungu wokoma mtima, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika, ndi wokhulupirika kotheratu. Mundiyang'ane ndipo mundichitire chifundo. Mundipatse mphamvu zanu ine mtumiki wanu, mundipulumutse ine mwana wa mdzakazi wanu. Mundiwonetse chizindikiro chakuti mumandikomera mtima, kuti odana nane achite manyazi. Adzaona kuti Inu Chauta mwandithandiza ndi kundilimbitsa mtima. Mzinda umene Chauta adamanga maziko ake, uli pa phiri loyera. Chauta amakonda mzinda wa Ziyoni amaukonda kupambana kwina kulikonse kumene zidzukulu za Yakobe zimakhala. Iwe mzinda wa Mulungu, anthu amakamba zambiri zotamanda iwe. Amati, “Pakati pa amene amandidziŵa, ndikutchula Rahabu ndi Babiloni. Ponena za dziko la Filistiya, Tiro ndi Etiopiya, anthu amati, ‘Uje adabadwira kumeneko.’ ” Koma ponena za Ziyoni adzati, “Onse adabadwira kumeneko,” chifukwa Wopambanazonse mwini wake ndiye amene adzaulimbitsa mzindawo. Tsono polemba maina a mitundu yonse ya anthu, Chauta adzati, “Wakutiwakuti adabadwira ku Ziyoni.” Oimba ndi ovina adzati, “Ziyoni ndiwe kasupe wa madalitso athu onse.” Inu Chauta, Mpulumutsi wanga, ndimalirira Inu usana ndi usiku, kuti mundithandize. Pemphero langa lifike kwa Inu, tcherani khutu kuti mumve kulira kwanga. Pakuti mtima wanga ndi wodzaza ndi mavuto, moyo wanga ukuyandikira ku malo a anthu akufa. Ndikuŵerengedwa pamodzi ndi anthu otsikira ku manda. Ndasanduka munthu wopanda mphamvu. Ndili ngati munthu womsiya yekha pakati pa anthu akufa, ngati munthu wophedwa amene wagona m'manda. Ndili ngati anthu amene Inu simuŵakumbukiranso, popeza kuti ndi ochotsedwa m'manja mwanu. Inu mwandiika pansi penipeni pa dzenje m'malo akuya a mdima wandiweyani. Mkwiyo wanu ukundipsinja, mukundimiza ndi mafunde anu onse. Inu mwachititsa kuti anzanga azindithaŵa, mwandisandutsa chinthu choŵanyansa. Ndatsekerezedwa kotero kuti sindingathe kuthaŵa. M'maso mwanga mwada ndi chisoni. Tsiku ndi tsiku ndimakuitanani, Inu Chauta, Ndimakweza manja anga kwa Inu. Kodi zodabwitsa mumachitira anthu akufa? Kodi iwowo nkuuka kuti akutamandeni? Kodi chikondi chanu chosasinthikacho amachilalikira ku manda? Kodi amasimba za kukhulupirika kwanu ku malo achiwonongeko? Kodi zodabwitsa zanu zimadziŵika mu mdima? Ndani angadziŵe za chithandizo chanu chopulumutsa m'dziko la anthu oiŵalika? Koma ine ndimalirira Inu Chauta, m'maŵa pemphero langa limakafika kwa Inu. Inu Chauta, chifukwa chiyani mukunditaya? Chifukwa chiyani mukundibisira nkhope yanu? Kuyambira ubwana wanga mpaka kukula, ndakhala ndikupirira zilango zanu pozunzika mpaka pafupi kufa, tsopano ndatheratu. Mkwiyo wanu wandimiza, moyo wanga waonongekeratu ndi ukali wanu woopsa. Zonsezi zimandizinga tsiku lonse ngati chigumula, zanditsekereza kwathunthu. Inu mwathaŵitsa anthu ondikonda ndi abwenzi anga, mdima wokha ndiye mnzanga amene wanditsalira. Inu Chauta, ndidzaimba mosalekeza nyimbo yotamanda chikondi chanu chosasinthika. Ndidzalalika ndi pakamwa panga za kukhulupirika kwanu ku mibadwo yonse. Chikondi chanu chosasinthika chakhazikika kuti chikhale mpaka muyaya, kukhulupirika kwanu nkwachikhalire ngati mlengalenga. Inu mwanena kuti, “Ndachita chipangano ndi wosankhidwa wanga, ndalumbira kwa Davide mtumiki wanga kuti, ‘Ndidzakhazikitsa zidzukulu zako mpaka muyaya, ndidzasungira mibadwo yonse mpando wako waufumu.’ ” Zakumwamba zimatamanda zodabwitsa zanu, Inu Chauta, zimatamanda kukhulupirika kwanu mu msonkhano wa oyera mtima. Kodi ndani mu mlengalenga angathe kulingana ndi Chauta? Ndani pakati pa akumwamba amafanafana naye? Mulungu ndiye amene amamuwopa mu msonkhano wa anthu oyera mtima, ndiye wamkulu ndi wolemekezeka pakati pa onse omzungulira. Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, kodi ndani ali wamphamvu ngati Inu Chauta, amene muli okhulupirika pa zonse? Mumalamulira nyanja yaukali. Mafunde ake akakwera, Inu mumaŵakhalitsa bata. Mudatswanya chilombo cha m'nyanja ndi kuchisandutsa mtembo. Mudabalalitsa adani anu ndi mkono wanu wamphamvu. Zakumwamba ndi zanu, dziko lapansi nalonso ndi lanu. Mudapanga dziko lonse ndi zonse zam'menemo. Mudalenga kumpoto ndi kumwera. Mapiri a Tabori ndi Heremoni akukutamandani ndi chimwemwe. Inu muli ndi mphamvu zonse. Dzanja lanu ndi lamphamvu kwambiri, dzanja lanu lamanja ndi lopambana. Maziko a ufumu wanu ndiwo kulungama ndi kuweruza mosakondera. Mumaonetsa chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika pa zonse zimene mumachita. Ngodala anthu amene mumaŵaphunzitsa kuimba nyimbo zachikondwerero, amene amayenda m'chikondi chanu, Inu Chauta. Iwowo amakondwa masiku onse chifukwa cha Inu, ndipo amatamanda kulungama kwanu. Amanyadira ulemerero wanu ndi mphamvu zanu. Mphamvu zathu zalimba chifukwa mwatikomera mtima. Chauta ndiye chishango chathu, Woyera wa Israele ndiye mfumu yathu. Kale mudalankhula m'masomphenya kwa anthu anu okhulupirika, mudati, “Ndamuveka chisoti chaufumu munthu amene ali wamphamvu, ndamukweza amene ali wosankhidwa pakati pa anthu. “Ndampeza Davide mtumiki wanga, ndamdzoza ndi mafuta anga oyera, “Kotero kuti dzanja langa lidzamchirikiza mpaka muyaya, mkono wanganso udzamulimbitsa. “Adani sadzampambana, anthu oipa sadzamtsitsa. Ndidzatswanya adani ake pamaso pake, ndi kukantha odana naye. “Kukhulupirika ndiponso chikondi changa chosasinthika zidzakhala naye, ndidzalimbitsa mphamvu zake, kuti mbiri yanga isungike. Ndidzakuza ufumu wake kuchokera ku Nyanja Yaikulu mpaka kukafika ku mtsinje wa Yufurate. “Iye adzandiwuza kuti, ‘Inu ndinu Atate anga, Mulungu wanga, Thanthwe londipulumutsa.’ Ndithu ndidzamsandutsa mwana wanga wachisamba, adzakhala wopambana mafumu a dziko lapansi. “Ndidzamkonda nthaŵi zonse ndi chikondi changa chosasinthika, chipangano changa ndi iye sichidzaphwanyika. Ndidzakhazikitsa zidzukulu zake pa mpando wachifumu, mpaka muyaya, ndipo ufumu wake udzakhala waukulu ngati mlengalenga. “Koma ngati ana ake asiya lamulo langa, ndipo satsata malangizo anga, ngati aphwanya malamulo anga, ndipo sasunga malangizo anga, “ndidzaŵalanga ndi ndodo, chifukwa cha zolakwa zao, ndidzaŵakwapula ndi zikoti chifukwa cha machimo ao. Koma Davide sindidzamchotsera chikondi changa chosasinthika, sindidzakhala wosakhulupirika kwa iye. “Sindidzaswa chipangano changa, kapena kusintha mau otuluka pakamwa panga. Ndidalumbira kamodzinkamodzi kuti, ‘Pali dzina langa loyera! Sindidzamnamiza Davide.’ “Zidzukulu zake sizidzatha mpaka muyaya, mpando wake wachifumu udzakhalapo nthaŵi zonse, monga m'mene likhalira dzuŵa pamaso panga. Ufumu wake udzakhazikika mpaka muyaya ngati mwezi, mboni yanga yokhulupirika mu mlengalenga.” Koma tsopano Inu mwamtaya ndi kumkana wodzozedwa wanu, mwamkwiyira kwambiri. Mwakana chipangano chanu ndi mtumiki wanu, mwadetsa m'fumbi chisoti chake chaufumu. Mwagumula makoma ake onse, mwasandutsa malinga ake mabwinja. Onse odutsa amamlanda zinthu zake, anzake amamunyodola. Mwalimbikitsa amaliwongo ake, mwakondwetsa adani ake onse. Inde, mwabunthitsa lupanga lake, ndipo simudamlimbitse pa nkhondo. Mwamchotsera ndodo yachifumu m'manja, ndipo mwataya pansi mpando wake wachifumu. Mwamkalambitsa msanga, mwamkuta ndi manyazi. Kodi mpaka liti, Inu Chauta? Kodi mudzandibisalira mpaka muyaya? Kumbukirani kuti masiku a moyo wanga ndi ochepa. Zoonadi, mudalenga anthu onse kuti akhale a moyo waufupi kwambiri. Kodi ndani angathe kukhala moyo osaona imfa? Ndani angathe kupulumutsa moyo wake polewa mphamvu za malo a anthu akufa? Ambuye, chili kuti chikondi chanu chosasinthika chakale chija, chimene mudachilumbirira Davide kuti mudzakhala wokhulupirika? Ambuye, kumbukirani kunyozedwa kwa mtumiki wanune, ndakhala ndikupirira chamumtima chipongwe cha anthu. Kumbukirani kuti amene akundinyozawo ndi adani anu, Inu Chauta, iwo akunyoza Wodzozedwa wanu paliponse pamene waponda. Chauta atamandike mpaka muyaya. Inde momwemo. Inde momwemo. Inu Ambuye, ndinu kothaŵira kwathu pa mibadwo yonse. Mapiri asanabadwe, ndipo musanalenge dziko lapansi ndi pokhala anthu, ndinu Mulungu kuyambira muyaya mpaka muyaya. Inu mumabwezera anthu ku fumbi, ndipo mumati, “Bwererani inu ana a anthu.” Pakuti zaka chikwi chimodzi pamaso panu zili ngati dzulo chabe, kapena ngati kamphindi chabe kausiku. Inu mumachotsa moyo wa anthu mwadzidzidzi. Ali ngati maloto, ali ngati udzu wongotsitsimuka m'maŵa. M'mamaŵamo umatsitsimuka ndipo umakondwa. Madzulo umafota ndi kuuma. Ife tapseratu ndi mkwiyo wanu woyaka, tikufa ndi mantha chifukwa cha ukali wanu. Inu mwaika machimo athu pamaso panu, ngakhale machimo obisika mwaŵaonetsa poyera. Pajatu masiku athu amachepa chifukwa cha mkwiyo wanu, zaka zathu zimatha ngati kuusa moyo chabe. Zaka za moyo wathu nzokwanira makumi asanu ndi aŵiri, tikakhala amphamvu, ndiye makumi asanu ndi atatu. Koma zaka zonsezo ndi za nkhaŵa ndi mavuto. Zakazo zimatha msanga, ife nkumapita. Kodi ndani amadziŵa kukula kwa mkwiyo wanu ndi ukali wanu, kupambana anthu okuwopani? Tsono tiphunzitseni kuŵerenga masiku athu, kuti tikhale ndi mtima wanzeru. Lezani mtima, Inu Chauta. Nanga mudzatikwiyira mpaka liti? Achitireni chifundo atumiki anu. Tidzazeni m'maŵa mulimonse ndi chikondi chanu chosasinthika, kuti tizikondwa ndi kusangalala masiku athu onse. Tisangalatseni masiku ambiri monga masiku amene mudatisautsira, zaka zambiri monga zaka zimene tidaona mavuto. Mulole kuti ntchito zanu ziwoneke kwa atumiki anu, mphamvu zanu zaulemerero ziwoneke kwa ana ao. Inu Ambuye, Mulungu wathu, mutikomere mtima, ndi kudalitsa zonse zimene timachita, ndithu mudalitse ntchito zonse za manja athu. Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe, adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.” Ndithu, Iye adzakupulumutsa ku msampha wa wosaka, ndiponso ku mliri woopsa. Adzakuphimba ndi nthenga za mapiko ake, udzapeza malo othaŵirako m'mapikomo. Kukhulupirika kwake kumateteza monga chishango ndi lihawo. Sudzachita mantha ndi zoopsa zausiku, kapena nkhondo nthaŵi yamasana. Sudzaopanso mliri wogwa usiku, kapena zoononga moyo masana. Anzako chikwi chimodzi angathe kuphedwa pambali pakopa, kapena zikwi khumi ku dzanja lako lamanja, koma iwe zoopsazo sizidzakukhudza. Uzingopenya ndi maso ako, ndipo udzaona m'mene amalangidwira anthu ochita zoipa. Chifukwa chakuti wavomera Chauta kuti akhale malo ako othaŵirako, wavomera Wopambanazonse kuti akhale malo ako okhalamo, zoipa sizidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi nyumba yako. Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite. Adzakunyamula m'manja mwao, kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala. Udzatha kuponda mkango ndi njoka, zoonadi udzaponda ndi phazi lako msona wa mkango ndiponso chinjoka. Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa. Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza. Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa. Nkwabwino kuthokoza Chauta, kuimba nyimbo zotamanda dzina lanu, Inu Wopambanazonse. Nkwabwino m'maŵa kulalika za chikondi chanu chosasinthika, ndipo usiku kusimba za kukhulupirika kwanu, poimba nyimbo zokoma ndi gitara, zeze ndi pangwe. Inu Chauta, mwandisangalatsa ndi ntchito zanu. Motero ndikufuula ndi chimwemwe chifukwa cha zimene Inu mwachita. Ntchito zanu si kukula kwake, Inu Chauta! Maganizo anu si kuzama kwake! Munthu wopanda nzeru sangadziŵe, munthu wopusa sangamvetse zimenezi, zakuti, ngakhale anthu oipa aziphuka ngati udzu, ndipo anthu ochimwa zinthu ziziŵayendera bwino, kwao nkuwonongeka kwamuyaya. Inu nokha Chauta, ndinu Wopambanazonse mpaka muyaya. Ndithudi adani anu, Inu Chauta, adani anu adzaonongeka, onse ochita zoipa adzamwazikana. Koma ine mwandilimbitsa ngati njati. Mwandidzoza ndi mafuta atsopano. Maso anga aona kuwonongeka kwa adani anga, makutu anga amva za kugwa kwa adani ondiwukira. Anthu okondweretsa Mulungu zinthu zimaŵayendera bwino ngati mitengo ya mgwalangwa, amakula ngati mikungudza ya ku Lebanoni. Ali ngati mitengo yookedwa m'Nyumba ya Chauta, yokondwa m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu wathu. Mitengoyi imabalabe zipatso ngakhale itakalamba, nthaŵi zonse imakhala ndi madzi ndipo imabiriŵira, imaonetsa kuti Chauta ndi wolungama. Iye ndiye thanthwe langa mwa Iye mulibe chokhota. Chauta ndiye mfumu. Wavala ulemerero, wavala mphamvu ngati lamba. Iye adakhazikitsa dziko lapansi, silidzagwedezeka konse. Mpando wanu waufumu, Inu Chauta, mudaukhazikitsa kuyambira makedzana, Inu ndinu amuyaya. Inu Chauta, nyanja zazikulu zakwera, zikukokoma koopsa. Mafunde ake akuchita mkokomo waukulu. Chauta amene ali pamwamba, ndi wamphamvu kupambana kulindima kwa madzi ambiri, ndi wamphamvu kuposa mafunde am'nyanja. Malamulo anu ndi osasinthika, Inu Chauta, Nyumba yanu ndi yoyera mpaka muyaya. Inu Chauta, ndinu Mulungu wolipsira, Inu Mulungu wolanga, dziwonetseni. Dzambatukani, Inu Muweruzi wa dziko lapansi, apatseni anthu onyada zoŵayenerera. Inu Chauta, kodi anthu oipa adzadzitamabe mpaka liti? Amalankhula modzikuza ndipo amanyadira zoipa zao. Amatswanya anthu anu, Inu Chauta, amazunza anthu anu osankhidwa. Amapha akazi amasiye ndi alendo okhala nawo m'dziko mwao, amaphanso ana amasiye. Kenaka amati, “Chauta sakuwona, Mulungu wa Yakobe sakuzidziŵa.” Mvetsani anthu opusa kwambirinu. Zitsiru inu, mudzakhala ndi nzeru liti? Kodi amene adalenga makutu, sangathe kumva? Kodi amene adapanga maso, sangathe kupenya? Kodi wolangiza mitundu ya anthu, sangathe kulanga? Kodi wophunzitsa anthu onse, alibe nzeru? Chauta amadziŵa maganizo a anthu kuti ndi mpweya chabe. Inu Chauta, ngwodala munthu amene mumamlangiza, amene mumamphunzitsa ndi malamulo anu. Mumampumitsa pa nthaŵi yamavuto, mpaka woipa ataloŵa m'dzenje. Chauta sadzaŵataya anthu ake, sadzaŵasiya okha osankhidwa ake. Chilungamo chidzaŵabwereranso kwa anthu ake, ndipo onse oongoka mtima adzachitsata. Ndani amalimba mtima kuti andimenyere nkhondo ndi anthu oipa? Ndani amaimira mbali yanga, kuti alimbane ndi anthu ochita zoipa? Chauta akadapanda kundithandiza, bwenzi posachedwa nditapita ku dziko lazii. Pamene ndinkaganiza kuti, “Phazi langa likuterereka,” nkuti chikondi chanu chosasinthika chikundichirikiza. Pamene nkhaŵa zikundichulukira, Inu mumasangalatsa mtima wanga. Kodi angathe kugwirizana nanu olamulira oipa, amene amapotoza malamulo anu olungama? Amagwirizana kuti aononge anthu osalakwa, nagamula kuti opanda mlandu aphedwe. Koma Chauta wasanduka linga langa londiteteza, Mulungu ndiye thanthwe langa lothaŵirako. Adzaŵalanga chifukwa cha machimo ao, adzaŵaononga chifukwa cha kuipa kwao, zoonadi, Chauta, Mulungu wathu, ndiye amene adzaŵafafanize. Bwerani, timuimbire Chauta. Tiyeni tifuule ndi chimwemwe kwa Iye, thanthwe lotipulumutsa. Tiyeni, tikafike pamaso pake, tikamthokoze, tiyeni tifuule kwa Iye ndi chimwemwe, timuimbire nyimbo zotamanda. Pakuti Chauta ndiye Mulungu wamkulu, ndiye Mfumu yaikulu yopambana milungu yonse. Maziko ozama a dziko lapansi ali m'manja mwake. Mapiri aatali omwe ngakenso. Nyanja ndi yake, popeza kuti ndiye adailenga. Mtunda ndi wakenso, popeza kuti ndiye adaupanga. Bwerani, timpembedze ndi kumlambira. Tiyeni tigwade pamaso pa Chauta Mlengi wathu. Pakuti ndiye Mulungu wathu, ndipo ife ndife anthu a pa busa lake, ndife nkhosa zodyera m'manja mwake. Lero mukadamverako mau ake! Musaumitse mitima yanu monga ku Meriba kuja, monganso tsiku lija ku Masa m'chipululu muja, pamene makolo anu adandiputa mondiyesa ngakhale anali ataona ntchito zanga. Pa zaka makumi anai ndidaipidwa ndi mbadwo umenewo, choncho ndidati, “Ameneŵa ndi anthu osakhulupirika, sasamalako njira zanga.” Choncho ndidakwiya nkulumbira kuti anthuwo sadzaloŵa ku malo anga ampumulo. Imbirani Chauta nyimbo yatsopano! Imbirani Chauta, anthu a m'dziko lonse lapansi! Imbirani Chauta, tamandani dzina lake! Lalikani za chipulumutso chake tsiku ndi tsiku. Lengezani za ulemerero wake kwa anthu a mitundu yonse, simbani za ntchito zake zodabwitsa kwa anthu a m'maiko onse. Chauta ngwamkulu, ngwoyenera kumtamanda kwambiri. Nwoyenera kumuwopa kupambana milungu yonse. Paja milungu yonse ya mitundu ina ya anthu ndi mafano chabe. Koma Chauta ndiye adalenga zakumwamba. Ulemu ndi ufumu zili pamaso pake. Mphamvu ndi kukongola zili m'Nyumba mwake. Tamandani, inu anthu a mitundu yonse, vomerezani kuti ulemerero ndi mphamvu, zonse nzake. Tamandani ulemerero wa dzina la Chauta. Bwerani ndi zopereka, ndipo muloŵe m'mabwalo a Nyumba yake. Pembedzani Chauta waulemerero ndi woyera, njenjemerani pamaso pake, inu anthu onse a pa dziko lapansi. Uzani mitundu ya anthu kuti, “Chauta ndiye Mfumu. Dziko lonse lidakhazikitsidwa molimba, silidzagwedezeka konse. Adzaweruza mitundu yonse ya anthu mwachilungamo.” Zakumwamba zisangalale, zapansi pano zikondwere, nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zam'menemo. Minda zikondwe pamodzi ndi zonse zam'menemo. Mitengo yam'nkhalango idzaimba mokondwa pamaso pa Chauta, pamene zabwera kudzalamulira dziko lapansi. Adzalamulira dziko lonse mwachilungamo, adzalamulira anthu a mitundu yonse moona. Chauta ndiye Mfumu, anthu a pa dziko lapansi akondwere, anthu onse a m'mbali mwa nyanja asangalale. Mitambo ndi mdima waukulu zamzinga Chauta. Amalamulira molungama, mu ufumu wake mulibe tsankho. Moto umapita patsogolo pake, umapsereza adani ake omzinga kulikonse. Zing'aning'ani zake zimaŵalitsa dziko lonse lapansi, dziko lonse limapenya nkugwedezeka. Mapiri amasungunuka ngati sera pamaso pa Chauta, ndiye wolamulira dziko lonse lapansi. Zakumwamba zimalalika za kulungama kwake, ndipo anthu a mitundu yonse amaona ulemerero wake. Onse opembedza milungu yonama, amene amanyadira mafano achabechabe, amachititsidwa manyazi, pakuti milungu ina yonse imagonjera Chauta. Anthu a ku Ziyoni akumva, ndipo akusangalala, midzi ya ku Yuda nayonso ikukondwera chifukwa cha kaweruzidwe kanu, Inu Chauta. Pakuti Inu Chauta ndinu Wopambanazonse, wolamulira dziko lonse lapansi. Ndinu amphamvu kupambana milungu yonse. Chauta amakonda anthu odana ndi zoipa. Iye amasunga moyo wa anthu ake oyera mtima. Amaŵapulumutsa kwa anthu oipa. Amaŵalira anthu amene amamumvera, ndipo anthuwo amakhaladi ndi chimwemwe. Inu ndi anthu a Chauta, kondwerani mwa iye, ndipo mumthokoze potchula dzina lake loyera. Imbirani Chauta nyimbo yatsopano, popeza kuti wachita zodabwitsa. Dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyera zampambanitsa. Chauta waonetsa kuti Iye wapambana pa nkhondo, waulula pamaso pa anthu a mitundu yonse kuti Iye ndi wolungama. Wakumbukira chikondi chake chosasinthika ndi kukhulupirika kwake pa fuko la Israele. Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu. Fuulirani Chauta ndi chimwemwe, inu dziko lonse lapansi. Muimbireni mokondwa nyimbo zotamanda. Imbani nyimbo zoyamika Chauta ndi pangwe, lizani pangwe ndi nyimbo zokoma. Imbirani Chauta Mfumu, imbani molimbika ndi malipenga ndi mbetete. Nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zam'menemo, dziko lifuule pamodzi ndi anthu onse am'menemo. Mitsinje iwombe m'manja, mapiri aimbe pamodzi mwachimwemwe pamene Chauta akufika, popeza kuti akubwera kudzaweruza dziko lapansi. Adzaweruza dziko lonse mwachilungamo, adzaweruza mitundu yonse mosakondera. Chauta ndiye mfumu, mitundu ya anthu injenjemere. Wakhala pa akerubi ngati pa mpando wake wachifumu. Dziko lapansi ligwedezeke! Chauta ndi wamkulu ku Ziyoni. Ali pamwamba pa mitundu yonse ya anthu. Onse atamande dzina lake lalikulu ndi loopsa! Iye ndi woyera! Ndinu Mfumu yamphamvu, yokonda chilungamo, mwakhazikitsa khalidwe losakondera ndiponso kuweruza kolungama m'dziko la Yakobe. Tamandani Chauta, Mulungu wathu, mpembedzeni ku mpando wake waufumu. Iye ndi woyera! Mose ndi aroni anali ena mwa ansembe ake, Samuele nayenso anali mmodzi mwa anthu otama dzina la Chauta mopemba. Ankalira kwa Chauta Iye nkumaŵayankha. Ankalankhula nawo mu mtambo woima kuti njo. Iwo ankasunga mapangano ndi malangizo amene Iye adaŵapatsa. Inu Chauta, Mulungu wathu, munkaŵayankha, munali Mulungu woŵakhululukira, komabe wolanga ntchito zao zoipa. Tamandani Chauta, Mulungu wathu, mpembedzeni ku phiri lake loyera. Chauta, Mulungu wathu, ndi woyera. Fuulani kwa Chauta ndi chimwemwe, inu maiko onse. Tumikirani Chauta mosangalala. Bwerani pamaso pake mukuimba mokondwa. Dziŵani kuti Chauta ndiye Mulungu. Ndiye amene adapanga ife, ndipo ifeyo ndife ake. Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake. Loŵani pa zipata zake mukuthokoza, pitani m'mabwalo a Nyumba yake mukutamanda. Yamikani Chauta, lemekezani dzina lake! Paja Iye ndi wabwino. Chikondi chake nchamuyaya, kukhulupirika kwake nkosatha. Ndidzaimba nyimbo zotamanda kukhulupirika ndi kulungama. Ndidzakuimbirani Inu Chauta. Ndidzatsata njira yopanda cholakwa. Nanga mudzabwera liti kwa ine? Ndidzakhala ndi mtima wangwiro m'nyumba mwanga. Sindidzaika maso anga pa chinthu chilichonse chachabechabe. Ndimadana ndi zochita za anthu okusiyani, sizindikomera konse. Ndidzakhala kutali ndi anthu a mtima woipa, sindidzalola choipa chilichonse kuloŵa mwa ine. Munthu wosinjirira mnzake kuseri ndidzamcheteketsa. Wooneka wonyada ndi wodzikuza sindidzamulekerera. Koma anthu okhulupirika am'dziko, ndidzaŵayang'ana moŵakomera mtima, ndipo adzakhala ndi ine. Oyenda m'njira yopanda cholakwa adzanditumikira. Palibe munthu wochita zonyenga amene adzakhale m'nyumba mwanga. Palibe munthu wolankhula zabodza amene adzakhale pafupi ndi ine. Tsiku ndi tsiku ndidzaononga oipa onse am'dziko. Onse ochita zoipa ndidzaŵachotsa mu mzinda wa Chauta. Inu Chauta, imvani pemphero langa, kulira kwanga kufike kwa Inu. Musandibisire nkhope yanu pa tsiku la mavuto anga. Tcherani khutu kuti mundimve, mundiyankhe msanga pa tsiku limene ndikukuitanani. Masiku anga amangopita ngati utsi, ndipo thupi langa likuyaka ngati ng'anjo. Mtima wanga wakanthidwa, ndipo wafota ngati udzu, zoonadi, ngakhale chakudya chimandinyansa. Ndaonderatu ngati munthu wachitopa, ntchito yanga ndi kubuula nthaŵi zonse. Ndili ngati mbalame yakuchipululu, ngati kadzidzi wam'mabwinja. Ndimagona osapeza tulo, ndili ngati mbalame yokhala yokha pa denga, Tsiku lonse adani anga amandichita chipongwe, onse ondinyoza amatchula dzina langa potemberera. Inetu ndimadya phulusa ngati chakudya, chakumwa changa ndimasakaniza ndi misozi, chifukwa cha ukali wanu ndi mkwiyo wanu, popeza kuti Inu mwandinyamula ndi kunditaya. Masiku anga ali pafupi kutha ngati mthunzi wamadzulo. Ndikufota ngati udzu. Koma Inu Chauta, mumakhala pa mpando wanu waufumu mpaka muyaya. Anthu a mibadwo yonse adzakukumbukirani. Mudzadzuka nkuchitira chifundo mzinda wa Ziyoni, zoonadi, nthaŵi yake youkomera mtima yafika. Mzindawo amaukondabetu anthu anu, ngakhale waonongeka ndi kusanduka bwinja. Mitundu ya anthu idzalemekeza Chauta moopa, mafumu onse a pa dziko lapansi adzaopa ulemerero wake. Chauta adzamanganso Ziyoni, ndipo adzaonekera mu ulemerero wake. Adzayankha pemphero la anthu ake otayika, sadzanyoza kupemba kwao. Zimenezi zilembedwe chifukwa cha mbadwo wakutsogolo, kuti anthu amene mpaka tsopano lino sanabadwebe, nawonso adzatamande Chauta, Iye adayang'ana pansi ali m'malo ake oyera kumwamba, ali kumwambako, Chauta adayang'ana pa dziko lapansi, kuti amve kubuula kwa anthu am'ndende, kuti aŵapulumutse amene adaayenera kuphedwa. Motero anthu adzalalika dzina la Chauta ku Ziyoni, ndipo adzamtamanda ku Yerusalemu, pamene mitundu ya anthu ndi mafumu adzasonkhana kuti apembedze Chauta. Chauta wathyola mphamvu zanga ndisanakule, wafupikitsa masiku anga. Ndikuti, “Mulungu wanga, musandichotse tsopano ndisanakalambe, Inu amene zaka zanu sizitha mpaka muyaya.” Inu mudaika maziko a dziko lapansi kalekale, ndipo zakumwamba mudazipanga ndi manja anu. Zonsezi zidzatha ngati malaya, koma Inu mulipobe. Inu mumazisintha ngati chovala, ndipo zimatha. Koma Inu simusintha, zaka zanu sizitha. Ana a ife atumiki anu adzakhala opanda nkhaŵa, zidzukulu zathu zidzakhazikika pamaso panu. Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, moyo wanga wonse umuyamike potchula dzina lake loyera. Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, ndipo usaiŵale zabwino zake zonse. Ndiye amene amakhululukira machimo ako onse, ndi kuchiritsa matenda ako onse. Ndiye amene amapulumutsa moyo wako ku manda. Amakuveka chikondi chake chosasinthika ndiponso chifundo chake ngati chisoti chaufumu. Ndiye amene amakupatsa zabwino nthaŵi zonse za moyo wako, choncho umakhalabe wa mphamvu zatsopano ngati mphungu. Chauta amaweruza mwachilungamo onse opsinjidwa amaŵachitira zolungama. Adadziŵitsa Mose njira zake, adaonetsa Aisraele ntchito zake. Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima, ndi wosakwiya msanga, ndipo chikondi chake chosasinthika nchachikulu. Akatikalipira, mkwiyo wake sudzakhala woyaka mpakampaka. Satilanga moyenerera machimo athu, satibwezera molingana ndi zolakwa zathu. Monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, ndi momwenso chidakulira chikondi chake chosasinthika kwa anthu oopa Chauta. Monga kuvuma kuli kutali ndi kuzambwe, ndi momwenso amachotsera zolakwa zathu kuti zikhale kutali ndi ife. Monga bambo amachitira chifundo ana ake, ndi momwenso Chauta amaŵachitira chifundo omulemekeza. Amadziŵa m'mene adatipangira, amakumbukira kuti ife ndife fumbi. Kunena za munthu, masiku ake sakhalitsa, ali ngati a udzu, munthuyo amakondwa ngati duŵa lakuthengo. Koma mphepo ikaombapo, duŵalo pamakhala palibe, siliwonekanso pa malo ake. Koma chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omumvera, zidzukulu zao zonse amazichitira zolungama. Anthuwo ndi amene amasunga chipangano chake, amene amakumbukira kusunga malamulo ake. Chauta wakhazikitsa mpando wake wachifumu kumwamba, ndipo amalamulira zonse mu ufumu wake. Tamandani Chauta, inu angelo ake, inu amphamvu amene mumamva mau ake, amene mumachita zimene amalamula. Tamandani Chauta, inu magulu a ankhondo ake onse, atumiki ake ochita zimene Iye afuna. Tamandani Chauta, inu zolengedwa zake zonse, ku madera onse a ufumu wake. Nawenso mtima wanga, tamanda Chauta! Tamanda Chauta, iwe mtima wanga. Inu Chauta, Mulungu wanga, ndinu aakulu kwambiri. Mumavala ulemu ndi ufumu. Mumadzifunditsa ndi kuŵala ngati chovala, mwatambasula mlengalenga ngati hema. Mwamanga Nyumba yanu pa madzi akumwamba, mitambo yaliŵiro ili ngati galeta lanu, mumayenda pa mapiko a mphepo, Mphepo mumazisandutsa amithenga anu, malaŵi amoto mumaŵasandutsa atumiki anu. Mudakhazika dziko lapansi pa maziko ake, kuti lisagwedezeke konse. Mudaliphimba ndi nyanja yozama ngati ndi chovala, ndipo madzi adakwera mpaka pamwamba pa mapiri. Mutaŵadzudzula, madziwo adathaŵa, atamva mkokomo wa bingu lanu, adamwazika. Mapiri adatumphuka, zigwa zidatsika, mpaka kumene Inu mudaakonzeratu. Madziwo Inu mudaŵaikira malire oti asabzole, kuti asaphimbenso dziko lapansi. Inu mumatumphutsa akasupe m'zigwa, mitsinje imayenda pakati pa mapiri. Imapatsa nyama zonse zakuthengo madzi akumwa, mbidzi zimapherapo ludzu. Mbalame zimamanga zisa pafupi ndi mitsinjeyo, zimaimba m'nthambi za mitengo. Inu mumathirira mapiri ndi madzi ochokera ku malo anu akumwamba. Dziko lapansi ladzaza ndi madalitso anu. Mumameretsa udzu kuti ng'ombe zidye, ndi zomera kuti munthu azilima ndi kupeza chakudya m'nthaka. Amapezamo vinyo wosangalatsa mtima wake, mafuta odzola kuti thupi lake lisisire, ndiponso buledi kuti ampatse mphamvu. Mitengo ya Chauta amaithirira ndi madzi ambiri, mikungudza ya ku Lebanoni imene adaibzala. Mbalame zimamanga zisa m'menemo, dokowe amamanga chisa m'mikungudzamo. M'mapiri aatali ndimo m'mene mumakhala mbalale, m'matanthwe ndimo m'mene mumathaŵira mbira. Inu mudapanga mwezi kuti uzisiyanitsa nyengo, ndipo dzuŵa limadziŵa nthaŵi yake yoloŵera. Mumapanga mdima nukhala usiku, ndipo nyama zam'nkhalango zimatuluka. Misona ya mikango imabangula pofunafuna nyama, kupempha chakudya kwa Mulungu. Dzuŵa likamatuluka, imabwerera nkukagona m'mapanga mwake. Munthu amapita ku ntchito yake, amakagwira ntchito mpaka madzulo. Inu Chauta ntchito zanu nzambiri, zonse mwazipanga mwanzeru, ndipo dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu. Kuli nyanja yaikulu ndi yotambalala, yodzaza ndi zinthu zosaŵerengeka, zinthu zamoyo, zazing'ono ndi zazikulu zomwe. Zombo zimayendamo pamodzi ndi Leviyatani, chilombo chija chimene mudachilenga kuti chiziseŵera m'madzimo. Zonse zolengedwa zimayang'anira kwa Inu, kuti muzipatse chakudya pa nyengo yake. Mukazipatsa zimachilandira; mukafumbatula dzanja lanu, zimakhuta. Mukazibisira nkhope yanu, zimachita mantha ndi kutaya mtima. Mukazichotsera mpweya, zimafa nkubwerera ku fumbi. Mukatumiza mpweya wanu zimalengedwa, ndipo mumakonzanso maonekedwe a dziko lapansi. Ulemerero wa Chauta ukhalebe mpaka muyaya, Chauta akondwe nazo ntchito zakezo, Iye amati akayang'ana dziko lapansi, limanjenjemera, akakhudza mapiri, mapiriwo amafuka nthunzi. Ndidzaimbira Chauta moyo wanga wonse. Ndidzaimba nyimbo zotamanda Chauta, nthaŵi zonse pamene ndili moyo. Mapemphero anga amkomere Chauta, popeza kuti ndimakondwa mwa Iye. Anthu ochimwa aonongeke pa dziko lapansi, anthu oipa asakhaleponso. Tamanda Chauta, iwe mtima wanga. Tamanda Chauta. Thokozani Chauta, tamandani dzina lake, lalikani za ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu. Imbirani Chauta, muimbireni nyimbo zomtamanda, lalikani za ntchito zake zodabwitsa. Munyadire dzina lake loyera. Ikondwe mitima ya anthu amene amapembedza Chauta. Muzidalira Chauta ndi mphamvu zake. Muziyesetsa kukhala pamaso pake kosalekeza. Inu zidzukulu za Abrahamu mtumiki wake, ana a Yakobe, osankhidwa ake, musaiŵale ntchito zodabwitsa ndi zozizwitsa zimene ankazichita, ndiponso m'mene ankaweruzira anthu. Iye ndiye Chauta, Mulungu wathu, amalamulira dziko lonse lapansi. Amasunga chipangano chake nthaŵi zonse, sangaiŵale lamulo limene adalipereka ku mibadwo yonse. Amasunga chipangano chimene adachita ndi Abrahamu, lonjezo lake limene adapatsa Isaki molumbira. Lonjezolo adabwerezanso kwa Yakobe kuti likhale chipangano chokhazikika mu Israele mpaka muyaya. Adati, “Ndidzakupatsa dziko la Kanani kuti likhale choloŵa chako chokhalira iweyo.” Pamene anali anthu oŵerengeka, anthu osatchuka, ongokhala nawo m'dzikomo, omangoyendayenda kuchokera ku mtundu wina wa anthu kupita ku mtundu wina, kuchokera ku ufumu wina kupita ku ufumu wina, sadalole ndi mmodzi yemwe kuti aŵapsinje, adalanga mafumu ena chifukwa cha anthu akewo. Adati, “Musakhudze odzozedwa anga, musaŵachite choipa aneneri anga.” Pamene Chauta adadzetsa njala m'dziko la Kanani ndi kuwononga chakudya chonse, Iye anali atatuma munthu patsogolo pa anthu ake, Yosefe uja amene adagulitsidwa ngati kapolo. Mapazi ake adapwetekedwa ndi matangadza, khosi lake lidavekedwa unyolo, mpaka zimene Yosefe adanena zija zidachitikadi. Mau a Chauta adatsimikiza kuti iye sadalakwe. Motero mfumu idalamula kuti akammasule, wolamulira mitundu ya anthuyo adammasuladi. Adamsandutsa mbuye wa nyumba yake, ndi wolamulira chuma chake chonse, kuti azilangiza nduna zake monga momwe ankafunira, ndi kuŵaphunzitsa nzeru akuluakulu. Tsono Israele adafika ku Ejipito. Yakobeyo adakhala nawo m'dziko la Hamu. Chauta adalola kuti anthu ake achuluke, naŵasandutsa amphamvu kupambana adani ao. Adaumitsa mitima ya adaniwo kuti adane ndi anthu ake ndi kuŵapanganirana zaupandu. Kenaka adatuma Mose mtumiki wake pamodzi ndi Aroni amene adamsankha. Iwo adachita zizindikiro m'dzina lake pakati pa anthuwo, adachita ntchito zozizwitsa m'dziko la Hamu. Chauta adatumiza mdima, nasandutsa dzikolo kuti likhale lamdima. Komabe anthuwo adakaniratu mau a Chauta. Iye adasandutsa madzi ao kukhala magazi, ndipo nsomba zao zidafa. Dziko lao lidadzaza ndi achule, ngakhale m'zipinda za mafumu zomwe. Adalankhula, ndipo kudatuluka ntchentche zochuluka, mtundu wa udzudzu udaloŵa m'dziko mwao monse. Adaŵagwetsera matalala m'malo mwa mvula, adaŵagwetsera ching'aning'ani chimene chinkang'anima m'dziko mwao monse. Adagwetsa mipesa yao ndi mikuyu yao, adathyola mitengo yonse ya m'dziko mwao. Adalankhula, ndipo kudafika dzombe ndi mandowa osaŵerengeka, amene adaononga zomera zonse za m'dziko mwao, nadya zipatso zonse za m'minda mwao. Iye adapha ana onse achisamba m'dziko mwao, ana onse oyamba, oŵabala akadali abiriŵiri. Kenaka Chauta adaŵatulutsa Aisraele atatenga siliva ndi golide, pakati pa mafuko awo panalibe amene adafooka. Aejipito adasangalala pamene iwo adapita, chifukwa ankachita nawo mantha anthuwo. Chauta adaika mtambo kuti uziphimba anthu ake, adaika moto kuti uziŵaunikira usiku. Iwo adapempha chakudya, ndipo Chauta adatumiza zinziri, adaŵapatsa buledi wambiri wochokera kumwamba. Adatsekula thanthwe, madzi nkutumphuka. Madziwo adayenda m'chipululu ngati mtsinje. Monsemo ankakumbukira lonjezo lake loyera limene adaachitira Abrahamu mtumiki wake. Motero Chauta adaŵatulutsa anthu ake, osankhidwa akewo adatuluka ndi chimwemwe akuimba. Adaŵapatsa maiko a mitundu ina ya anthu, adalanda minda ya anthu ena kuti ikhale yao. Potero Chauta adafuna kuti anthu ake azisunga malangizo ndi kumatsata malamulo ake onse. Tamandani Chauta! Tamandani Chauta. Thokozani Chauta chifukwa ngwabwino, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Ndani angathe kufotokoza za ntchito zamphamvu za Chauta, ndani angathe kumtamanda kokwanira? Ngodala anthu otsata malamulo a Chauta, anthu ochita zolungama nthaŵi zonse. Chauta, mundikumbukire pamene mukukomera mtima anthu anu. Mundithandize pamene mukuŵapulumutsa, kuti ndiwone zokoma za osankhidwa anu, kuti ndigaŵane nawo chisangalalo cha mtundu wanu, kuti ndipeze ulemerero pamodzi ndi anthu anu. Ife tachimwa monga makolo athu, tachita zoipa, sitidachite zabwino. Pamene makolo athu anali ku Ejipito, sadasamale ntchito zanu zodabwitsa. Sadakumbukire kukula kwa chikondi chanu chosasinthika, koma adaukira Mulungu Wopambanazonse ku Nyanja Yofiira kuja. Komabe Iye adaŵapulumutsa malinga ndi ulemerero wa dzina lake, kuti aonetse mphamvu zake zazikulu. Adalamula Nyanja Yofiira, ndipo idauma, adaŵatsogolera m'Nyanja yakuya, iwo nkuyenda pouma. Motero adaŵapulumutsa kwa amaliwongo, naŵalanditsa ku mphamvu za adani ao. Ndipo madzi adamiza adani ao onse, sadatsalepo ndi mmodzi yemwe. Tsono anthu ake adakhulupirira mau ake, naimba nyimbo zomtamanda. Koma posachedwa iwo adaiŵala ntchito zake, ndipo sadayembekeze malangizo ake. Adadzilekerera potsata zilakolako zao m'chipululu muja, adayesa Mulungu m'chipululumo. Iye adaŵapatsa zimene iwo adapempha, koma adatumiza nthenda yoopsa pakati pao. Nthaŵi ina anthuwo adaachitira kaduka Mose ndi Aroni, mtumiki wopatulika wa Chauta. Pamenepo nthaka idang'ambika nkumeza Datani, ndipo idakwirira gulu la Abiramu. Moto nawonso udabuka m'gulu mwao, malaŵi a moto adapsereza anthu oipawo. Iwo adapanga mwanawang'ombe ku Horebu, napembedza chifano chosungunula. Adasinthanitsa ulemerero wa Mulungu ndi chifano cha ng'ombe imene imadya udzu. Adaiŵala Mulungu Mpulumutsi wao amene adachita zinthu zazikulu ku Ejipito, ntchito zodabwitsa m'dziko la Hamulo, ndiponso zinthu zoopsa ku Nyanja Yofiira kuja. Nchifukwa chake adaŵauza kuti akadaŵaononga, pakadapanda Mose wosankhidwa wake kuima pamaso pake, ndi kuletsa mkwiyo wake kuti usaŵaononge. Motero iwo adanyoza dziko lokoma, chifukwa sadakhulupirire malonjezo ake. Adang'ung'udza m'mahema mwao ndipo sadamvere mau a Chauta. Nchifukwa chake Iye adakweza dzanja lake nalumbira kuti anthuwo adzafera m'chipululu, ndipo kuti adzamwaza zidzukulu zao pakati pa mitundu ina, ndi kuzibalalitsa m'maikom'maiko. Anthuwo adayamba kupembedzanso Baala wa ku Peori, ndi kumadya nawo nsembe zoperekedwa kwa anthu akufa. Motero adaputa mkwiyo wa Chauta ndi zochita zaozo, ndipo mliri udabuka pakati pao. Tsono Finehasi, atalanga olakwa, mliri uja udaleka. Motero iyeyo adaŵerengedwa kuti ndi wolungama ku mibadwo yonse mpaka muyaya. Anthuwo adakwiyitsa Chauta ku madzi a Meriba kuja, ndipo zinthu sizidamuyendere bwino Mose chifukwa cha anthuwo. Iwo adampsetsa mtima kwambiri, kotero kuti Moseyo adalankhula mosalingalira. Iwo sadaonongeretu mitundu ina ya anthu monga m'mene Chauta adaaŵalamulira, koma adasakanizana ndi mitundu inayo naphunzira kuchita zoipa zomwe anthu enawo ankachita. Adatumikira mafano ao amene adasanduka msampha kwa iwo. Adapereka nsembe ana ao aamuna ndi aakazi kwa mizimu yoipa. Adakhetsa magazi osachimwa, magazi a ana ao aamuna ndi aakazi, amene adaŵapereka nsembe kwa mafano a ku Kanani, choncho dzikolo adaliipitsa ndi imfa zimenezo. Adadzidetsa ndi ntchito zao, nakhala osakhulupirika pa zochita zao ngati mkazi wachigololo. Tsono mkwiyo wa Chauta udayakira anthu ake, chifukwa adanyansidwa nawo anthu akewo. Adaŵapereka kwa mitundu ina ya anthu, kotero kuti amene ankadana nawo, ndiwo amene ankaŵalamulira. Adani ao ankaŵazunza, ataŵagonjetsa adaŵaika mu ulamuliro wao. Nthaŵi zambiri Iye ankaŵapulumutsa, koma iwo ankamuukirabe osaleka, namamira m'machimo ao, Komabe Chauta adaŵathandiza pa mavuto ao pamene adamva kulira kwao. Adakumbukira chipangano chake chifukwa cha kuŵakonda anthuwo, naleza mtima chifukwa cha kukula kwa chikondi chake chosasinthika. Chauta adafeŵetsa mitima ya adani onse amene adagwira anthu ake ukapolo, kuti aŵachitire chifundo anthu akewo. Tipulumutseni Inu Chauta, Mulungu wathu, mutisonkhanitse kuchokera pakati pa anthu akunja, kuti tikuthokozeni potchula dzina lanu loyera, kuti tizinyadira pokutamandani. Atamandike Chauta, Mulungu wa Aisraele, kuyambira muyaya mpaka muyaya. Anthu onse anene kuti, “Inde momwemo.” Tamandani Chauta! Thokozani Chauta chifukwa ngwabwino, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Anenedi choncho oomboledwa a Chauta, amene Iye waŵapulumutsa ku mavuto. Waŵasonkhanitsa kuchokera ku maiko onse, kuchokera kuvuma ndi kuzambwe, kumpoto ndi kumwera. Ena adasokera m'chipululu, osapeza njira yopita ku mzinda woti akakhalemo. Adamva njala ndi ludzu, moyo wao unkafookeratu. Tsono anthu aja adalira kwa Chauta pamene anali m'mavuto amenewo, ndipo Chauta adaŵapulumutsa. Adaŵatsogolera pa njira yolunjika mpaka anthuwo adakafika ku mzinda woti akakhalemo uja. Athokoze Chauta chifukwa cha chikondi chake chosasinthika, chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa kwa anthu onse. Chauta amapha ludzu la munthu womva ludzu, amamudyetsa zinthu zabwino munthu womva njala. Ena adakhala mu mdima ali ndi chisoni, anali am'ndende ozunzika m'maunyolo achitsulo, pakuti adaatsutsa mau a Mulungu, adaakana monyoza malangizo a Wopambanazonse. Iye adaŵapsinja ndi ntchito yakalavulagaga, motero iwo adagwa pansi, popanda mmodzi woŵathandiza. Tsono anthu aja adalira kwa Chauta pamene anali m'mavuto amenewo, ndipo Chauta adaŵapulumutsa ku mavuto aowo. Chauta adaŵatulutsa anthuwo mu mdima ndi m'chisoni muja, ndipo adadula maunyolo ao. Athokoze Chauta chifukwa cha chikondi chake chosasinthika, chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa kwa anthu onse. Pajatu adathyola zitseko zamkuŵa, nadula paŵiri mipiringidzo yachitsulo. Ena adadwala chifukwa cha njira zao zoipa, nazunzika chifukwa cha machimo ao. Sankafuna chakudya cha mtundu uliwonse, ndipo adayandikira ku zipata za imfa. Tsono anthu aja adalira kwa Chauta pamene anali m'mavuto amenewo, ndipo Chauta adaŵapulumutsa ku mavuto aowo. Chauta adatumiza mau ake, naŵachiritsa anthuwo, adaŵapulumutsa kuti asaonongeke. Athokoze Chauta chifukwa cha chikondi chake chosasinthika, chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa kwa anthu onse. Apereke nsembe zothokozera, ndi kulalika ntchito za Chauta, poimba nyimbo zachimwemwe. Ena adakayenda ku nyanja m'zombo, namachita malonda pa Nyanja yaikulu. Adaona ntchito za Chauta, ntchito zake zodabwitsa, pa madzi akuya. Ndiye kuti Chauta adalamula nautsa namondwe amene adaŵindula mafunde apanyanja. Zombozo zidakwera mpaka m'mwamba nkutsikiranso kwakuya, ndipo anthuwo adataya mtima pa mavuto aowo. Adachita chizungulire namadzandira ngati anthu oledzera, kenaka nkuthedwa nzeru. Tsono anthu aja adalira kwa Chauta pamene anali m'mavuto amenewo, ndipo Chauta adaŵapulumutsa ku mavuto aowo. Chauta adatontholetsa namondwe, ndipo mafunde apanyanja adachita bata. Choncho anthuwo adasangalala chifukwa kudachita bata, ndipo Chauta adakaŵafikitsa kudooko kumene ankalinga. Athokoze Chauta chifukwa cha chikondi chake chosasinthika, chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa kwa anthu onse. Amtamande pa msonkhano wa anthu, amuyamike pa bwalo la akuluakulu. Adasandutsa mitsinje kuti ikhale chipululu, adasandutsa akasupe a madzi kuti akhale nthaka youma, dziko lachonde adalisandutsa nthaka yamchere, chifukwa cha kuipa kwa anthu okhala m'menemo. Komanso adasandutsa chipululu kuti chikhale ndi maiŵe a madzi, nthaka youma kuti ikhale akasupe a madzi. Ndipo kumeneko Chauta adakhazikako anthu anjala, tsono anthuwo adamanga mzinda woti azikhalamo. Adafesa mbeu m'minda, namaoka mipesa, ndipo adakolola dzinthu dzambiri. Chifukwa cha madalitso a Chauta, anthuwo adachuluka kwambiri, Chauta sadalole kuti zoŵeta za anthuwo zichepe. Pamene anthu ake chiŵerengero chao chidachepa, ndipo pamene adatsitsidwa chifukwa cha mazunzo, mavuto ndi chisoni, apo Chauta adagwetsa manyozo pa mafumu oŵapsinja naŵasokeretsa, m'chipululu. Koma anthu osoŵa adaŵatulutsa m'mavuto ao, adachulukitsa mabanja ao ngati magulu a nkhosa. Anthu olungama mtima amaona zimenezo, nkumasangalala, koma oipa onse amaŵakhalitsa chete. Munthu aliyense wanzeru asamale zimenezi, anthu alingalire za chikondi chosasinthika cha Chauta. Inu Mulungu, mtima wanga wakonzeka, ndithu, mtima wanga wakonzekadi! Ndidzaimba nyimbo, nyimbo yake yotamanda. Lumpha, iwe mtima wanga. Inu zeze ndi pangwe, tiyeni lirani. Ndidzadzutsa dzuŵa ndi nyimbo zanga. Ndidzakuthokozani, Inu Chauta, pakati pa mitundu ya anthu. Ndidzaimba nyimbo zokutamandani pakati pa anthu a m'maiko onse, pakuti chikondi chanu chosasinthika nchachikulu, chofika mpaka pamwamba pa mlengalenga, kukhulupirika kwanu kumafika mpaka ku mitambo. Inu Mulungu, onetsani ukulu wanu mumlengalenga monse. Wanditsani ulemerero wanu pa dziko lonse lapansi. Tipambanitseni pa nkhondo ndi dzanja lanu lamanja, mundiyankhe kuti ife, okondedwa anu, tipulumuke. Mulungu ali ku malo ake oyera, walonjeza kuti, “Ndidzakugaŵirani dziko la Sekemu mokondwa, ndidzakulemberani malire m'chigwa cha Sukoti. “Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanga. Efuremu ali ngati chisoti changa chodzitetezera. Yuda ali ngati ndodo yanga yaufumu. “Mowabu adzakhala ngati mbale yosambiramo ine. Edomu adzakhala poponda nsapato zanga. Ndidzafuula mokondwa nditagonjetsa Filistiya.” Ndani adzandifikitse ku mzinda wamalinga? Ndani adzanditsogolere ku Edomu? Si wina ai koma ndinu Mulungu amene mwatitaya, ndinu Mulungu amene mwaleka kuperekeza ankhondo athu. Tithandizeni kulimbana ndi adani athuwo, pakuti chithandizo cha munthu nchopandapake. Mulungu akakhala nafe, tidzamenya nkhondo molimba mtima, pakuti ndiye amene adzapondereza adani athu. Musakhale chete, Inu Mulungu, amene ndimakutamandani, pakuti anthu oipa ndi onama amakamba zondiwukira, amalankhula zondinamizira. Ponseponse amandilankhula mau achidani, amandinena popanda chifukwa. M'malo mwa chikondi changa, iwo amandibwezera zondineneza, ngakhale pamene ndikuŵapempherera. Motero amandibwezera zoipa m'malo mwa zabwino, amandiwonetsa chidani m'malo mwa chikondi changa. Sankhulani munthu woipa kuti aweruze mlandu wa wondiwukirayo, iye aimbidwe mlandu ndi munthu woneneza anzake. Pomuweruza apezeke kuti ali ndi mlandu, mapemphero ake akhale ngati kupalamula. Masiku ake akhale oŵerengeka, wina alandire udindo wake. Ana ake akhale amasiye, ndipo mkazi wake akhale mfedwa. Ana ake azingoyendayenda nkumapemphapempha, apirikitsidwe m'mabwinja m'mene amakhala. Wokongoza ndalama amlande zonse zimene ali nazo. Alendo afunkhe zimene adapindula ndi ntchito yake. Pasapezeke ndi mmodzi yemwe womukomera mtima, kapena wina woŵachitira chifundo ana ake amasiye aja. Zidzukulu zake zithe nkufa, dzina lao lisamvekenso mu mbadwo wachiŵiri. Chauta asaiŵale machimo a makolo ake, machimo a mai wake asafafanizike. Chauta asakhululukire machimowo mpaka muyaya, anthuwo aiŵalike pa dziko lapansi. Pakuti munthuyo sadakumbukire kuchita chifundo, koma adazunza osauka, osoŵa ndi ovutika mu mtima, mpaka kuŵapha. Ankakonda kutemberera, choncho matemberero amgwere. Sadakonde kudalitsa anthu ena, choncho madalitso akhale kutali ndi iye. Kutemberera anzake kunali ngati chovala chake, motero matemberero amgwere ngati mvula. Akhale ngati mafuta oloŵa m'mafupa mwake. Matemberero akhale ngati mwinjiro wofundira, ngati lamba wovala tsiku ndi tsiku. Zimenezi zikhale chilango chochokera kwa Chauta kugwera ondineneza. Ziŵagwere amene amalankhula zoipira moyo wanga. Koma Inu Mulungu, Ambuye anga, munditchinjirize malinga ndi ulemerero wa dzina lanu, mundipulumutse chifukwa chikondi chanu chosasinthika ndi chabwino. Pakuti ine ndine wosauka ndi wosoŵa, ndipo mtima wanga ukuŵaŵa kwambiri. Ndazimirira ngati mthunzi wamadzulo, ndapirikitsidwa ngati dzombe. Maondo anga afooka chifukwa chosala zakudya, thupi langa laonda ndi mutu womwe. Ondineneza amandinyodola, akandiwona amapukusa mitu yao. Thandizeni Chauta, Mulungu wanga. Pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika. Adani adziŵe kuti limeneli ndi dzanja lanu londipulumutsa, Inu Chauta, ndinu amene mwachita zimenezi. Iwo atemberere, koma Inu mundidalitse. Ondiputa muŵachititse manyazi, koma ine mtumiki wanu ndisangalale. Ondineneza akhale onyozeka, manyazi ao aŵakute ngati chovala. Ndidzathokoza Chauta kwambiri polankhula. Ndidzamtamanda pakati pa gulu la anthu. Paja Chauta amaimirira pafupi ndi munthu wosoŵa, amafuna kumpulumutsa kwa anthu ogamula kuti iyeyo aphedwe. Chauta adauza Mbuye wanga kuti, “Khala ku dzanja langa lamanja, mpaka nditasandutsa adani ako kukhala ngati chopondapo mapazi ako.” Chauta adzakuza ufumu wako wamphamvu kuchokera ku Ziyoni. Adzati, “Khala mfumu yolamulira adani ako.” Anthu ako adzadzipereka mwaufulu, pa tsiku limene udzaonetse mphamvu zako pa phiri loyera. Anyamata ako adzabwera kwa iwe mu unyinji wao, monga m'mene mame amabwerera m'mamaŵa. Chauta walumbira ndipo sadzasintha maganizo ake akuti, “Ndiwe wansembe mpaka muyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.” Ambuye ali pambali pako. Adzaphwanya mafumu pa tsiku la mkwiyo wao. Adzalanga mitundu ya anthu akunja, adzadzaza dziko lapansi ndi mitembo. Adzagonjetsa olamulira a pa dziko lonse lapansi. Adzamwa mu mtsinje wam'njira, ndipo adzaŵeramutsa mutu monyadira. Tamandani Chauta. Ndidzathokoza Chauta ndi mtima wanga wonse pa msonkhano wa anthu olungama mtima. Ntchito za Chauta nzazikulu, onse okondwera nazo amazilingalira. Ntchito zake ndi zaulemu ndi zaufumu, ndipo kulungama kwake nkwamuyaya. Amatikumbutsa ntchito zake zodabwitsa, Chauta ndi wokoma ndi wachifundo. Amapatsa chakudya anthu omuwopa, amakumbukira chipangano chake nthaŵi zonse. Amaonetsa anthu ake mphamvu za ntchito zake, poŵapatsa choloŵa cha anthu a mitundu ina. Ntchito za manja ake nzokhulupirika ndi zolungama. Malamulo ake onse ndi okhulupirika. Ndi okhazikika mpaka muyaya, paja adaŵapereka ndi mtima wokhulupirika ndi wolungama. Adapulumutsa anthu ake. Adakhazikitsa chipangano chake kuti chikhale chamuyaya. Dzina lake ndi loyera ndi loopsa. Kuwopa Chauta ndiye chiyambi cha nzeru. Wotsata malamulo ake amakhala ndi nzeru zenizeni. Chauta ndi wotamandika mpaka muyaya. Tamandani Chauta! Ngwodala munthu woopa Chauta, wokonda kusunga malamulo ake. Zidzukulu zake zidzakhala zamphamvu pa dziko lapansi. Ana a munthuyo adzakhala odala. Banja lake lidzakhala lachuma ndi lolemera, ndipo kulungama kwake kudzakhala kwamuyaya. Ngakhale nthaŵi ya mdima, munthu wochita chilungamo ayenda m'kuŵala, chifukwa ngwokoma mtima, wachifundo ndi woongoka. Munthu amene amakongoza mosafuna phindu, amene amayendetsa ntchito zake mwachilungamo, zinthu zimamuyendera bwino. Pakuti munthu wochita chilungamo sadzagwedezeka konse, sadzaiŵalika mpaka muyaya. Saopa akamva zoipa zimene zachitika. Mtima wake ndi wosasinthika, amakhulupirira Chauta. Ali wolimba mtima, sadzachita mantha, potsiriza adzaona adani ake atagonja. Amapereka chithandizo mwaufulu, amaoloŵa manja kwa anthu osauka. Chilungamo chake chidzakhala chamuyaya, adzakhala wamphamvu ndipo anthu adzampatsa ulemu. Munthu woipa amaona zimenezi, ndipo amapsa nazo mtima. Amakukuta mano nazimirira. Zokhumba za munthu woipa sizidzachitika konse. Tamandani Chauta! Mtamandeni, inu atumiki ake, tamandani dzina la Chauta. Yamikani Chauta kuyambira tsopano mpaka muyaya. Dzina la Chauta litamandike kuyambira ku matulukiro a dzuŵa mpaka ku maloŵero ake. Chauta akulamulira anthu a mitundu yonse, ulemerero wake ndi waukulu kuposa wa mlengalenga. Ndani angalingane ndi Chauta, Mulungu wathu, amene akukhala kumwamba, wochita kuŵeramira pansi poyang'ana mlengalenga ndi dziko lapansi. Amakweza munthu wosauka kuchokera ku fumbi, ndipo amatulutsa ku dzala anthu osoŵa. Amaŵakhazika pamodzi ndi mafumu, mafumu a anthu a Chauta. Amapatsa banja mkazi wosabala, namsandutsa mai wosangalala wa ana. Tamandani Chauta! Pamene Israele adatuluka ku Ejipito, pamene banja la Yakobe lidatuluka kuchokera ku mtundu wa anthu a chilankhulo chachilendo, Yuda adasanduka malo opatulika a Chauta, Aisraele adasanduka anthu a mu ufumu wake. Nyanja idaona zimenezi nithaŵa, mtsinje wa Yordani udabwerera m'mbuyo. Mapiri aakulu adalumphalumpha ngati nkhosa zamphongo, nazonso zitunda zidalumpha ngati anaankhosa. Iwe nyanja, chikukuvuta nchiyani kuti uzithaŵa? Nanga iwe Yordani, ukubwerereranji m'mbuyo? Inu mapiri, chikukuvutani nchiyani, kuti muzilumphalumpha ngati nkhosa zamphongo? Nanga inu zitunda, mukulumphiranji ngati anaankhosa? Njenjemera iwe dziko lapansi, chifukwa Chauta akubwera, zoonadi, akubwera Mulungu wa Yakobe. Iye amasandutsa thanthwe kukhala dziŵe lamadzi, amasandutsa mwala wolimba kukhala kasupe wa madzi. Kwa ife ai, Chauta, kwa ife ai, koma kwa dzina lanu lokha ndiye kukhale ulemerero. Chifukwa ndinu Mulungu wa chikondi chosasinthika ndi wokhulupirika. Chifukwa chiyani mitundu ina ya anthu iziti, “Mulungu wao ali kuti?” Mulungu wathu ali kumwamba, amachita chilichonse chimene afuna. Koma mafano ao ndi asiliva ndi agolide, opangidwa ndi manja a anthu. Pakamwa ali napo, koma salankhula. Maso ali nawo, koma sapenya. Makutu ali nawo, koma saamva. Mphuno ali nazo, koma sanunkhiza. Manja ali nawo, koma akakhudza, samva kanthu. Miyendo ali nayo, koma sayenda, ndipo satulutsa ndi liwu lomwe kukhosi kwao. Anthu amene amapanga mafanowo amafanafana nawo, chimodzimodzi onse amene amaŵakhulupirira. Iwe Israele, khulupirira Chauta. Chauta ndiye mthandizi wako ndi chishango chako. Iwe banja la Aroni khulupirira Chauta. Chauta ndiye mthandizi wako ndi chishango chako. Inu amene mumaopa Chauta, mkhulupirireni. Chauta ndiye mthandizi wanu ndi chishango chanu. Chauta watikumbukira ndipo adzatidalitsa. Adzadalitsa anthu a Israele, adzadalitsa banja la Aroni. Adzadalitsa amene amamlemekeza, anthu wamba ndi apamwamba omwe. Chauta akudalitseni inu, pamodzi ndi zidzukulu zanu zomwe. Akudalitseni Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi. Kumwamba nkwa Chauta, koma dziko lapansi adapatsa anthu. Akufa satamanda Chauta otsikira ku dziko lachete satamanda Chauta. Koma ife tidzatamanda Chauta kuyambira tsopano mpaka muyaya. Tamandani Chauta! Ndimakonda Chauta chifukwa amamva mau anga omupemba. Iye amatchera khutu kuti andimve, nchifukwa chake ndidzampempha nthaŵi zonse pamene ndili moyo. Misampha ya imfa idandizinga, zoopsa za m'dziko la akufa zidandigwera. Ndidaona mavuto, nkugwidwa ndi nthumanzi. Tsono ndidapemphera potchula dzina la Chauta kuti, “Chauta ndikukupemphani, pulumutsani moyo wanga.” Chauta ndi wokoma mtima ndi wolungama. Mulungu wathu ndi wachifundo. Chauta amasunga a mtima wodzichepetsa. Pamene ndidagwa m'zoopsa, Iye adandipulumutsa. Iwe mtima wanga, bwerera ku malo ako opumulira, chifukwa Chauta wakuchitira zokoma. Pakuti Inu Chauta, mwandipulumutsa ku imfa, mwaletsa misozi yanga, mwanditeteza kuti ndisaphunthwe. Ndimayenda pamaso pa Chauta m'dziko la amoyo. Ndidakhulupirirabe ngakhale pamene ndinkati, “Ndazunzika koopsa.” Pamene ndinkachita mantha, ndidati, “Anthu ndi osakhulupirika.” Ndidzambwezera chiyani Chauta pa zabwino zonse zimene adandichitira? Ndidzakweza chikho cha chipulumutso, ndidzapemphera potchula dzina la Chauta. Ndidzachita zimene ndidalumbira kwa Chauta pamaso pa anthu ake onse. Imfa ya anthu oyera mtima a Chauta, ndi yamtengowapatali pamaso pake. Chauta, ine ndine mtumiki wanu, mtumiki wanu weniweni, mwana wa mdzakazi wanu. Inu mwamasula maunyolo anga. Ndidzapereka kwa Inu nsembe yothokozera, ndidzapemphera potchula dzina la Inu, Chauta. Ndidzachita zimene ndidalumbira kwa Chauta pamaso pa anthu ake onse. Ndidzazipereka m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu, mu mzinda wa Yerusalemu. Tamandani Chauta! Tamandani Chauta, inu mitundu yonse ya anthu. Mlemekezeni kwambiri, inu anthu a m'maiko onse. Pakuti chikondi chake kwa ife nchachikulu, kukhulupirika kwa Chauta nkwamuyaya. Tamandani Chauta! Thokozani Chauta chifukwa ngwabwino, ndipo chikondi chake nchamuyaya. Aisraele anene kuti, “Chikondi chake nchamuyaya.” Banja la Aroni linene kuti, “Chikondi chake nchamuyaya.” Anthu oopa Chauta anene kuti, “Chikondi chake nchamuyaya.” Pamene ndinali m'mavuto ndidapemphera kwa Chauta, ndipo Iye adandichotsera mavutowo. Chauta akakhala pa mbali yanga, sindichita mantha. Munthu angandichite chiyani? Chauta ali pa mbali yanga kuti andithandize. Odana nane ndidzaŵayang'ana monyoza nditaŵapambana. Kuthaŵira kwa Chauta nkwabwino kupambana kukhulupirira munthu. Kuthaŵira kwa Chauta nkwabwino kupambana kukhulupirira mafumu. Adani a mitundu yonse adandizinga, koma ndidaŵaononga ndi mphamvu za dzina la Chauta. Adandizinga, inde adandizinga pa mbali zonse, koma ndidaŵaononga ndi mphamvu za dzina la Chauta. Adandizinga ngati njuchi, koma adatha msanga ngati moto wapaminga. Ndidaŵaononga ndi mphamvu za dzina la Chauta. Adandikankha kwambiri, kotero kuti ndinali pafupi kugwa, koma Chauta adandithandiza. Chauta amene ndimamuimbira ndiye mphamvu zanga. Ndiye mpulumutsi wanga. Mverani nyimbo m'mahema mwa anthu a Mulungu, nyimbo zokondwerera kupambana, zakuti, “Dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu, dzanja lamanja la Chauta lapambana, dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu.” Sindidzafa, ndidzakhala moyo, ndipo ndidzalalika ntchito za Chauta. Chauta wandilanga koopsa, koma sadandisiye kuti ndife. Tsekulireni zipata za Nyumba ya Mulungu, kuti ndifike ku malo ake achilungamo, ndikathokoze Chauta. Ichi ndicho chipata cha Chauta, anthu okhawo ochita chifuniro chake adzaloŵera pamenepa. Ndikukuyamikani popeza kuti mwandiyankha, ndipo mwasanduka Mpulumutsi wanga. Mwala umene amisiri omanga nyumba adaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya. Chauta ndiye amene wachita zimenezi, zimenezi nzodabwitsa pamaso pathu. Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli. Tipulumutseni, tikukupemphani Inu Chauta. Chauta, tikukupemphani kuti zinthu zitiyendere bwino. Ngwodala amene alikudza m'dzina la Chauta. Tikufunirani madalitso ochokera m'nyumba ya Chauta. Chauta ndi Mulungu, ndipo watipatsa kuŵala. Yambani mdipiti wachikondwerero mutatenga nthambi, mpaka kukafika ku guwa lansembe. Inu ndinu Mulungu wanga, ndidzakuthokozani. Inu ndinu Mulungu wanga, ndidzakutamandani. Thokozani Chauta pakuti ngwabwino, ndipo chikondi chake chosasinthika nchamuyaya. Ngodala amene moyo wao ulibe choŵadzudzulira, amene amayenda motsata malamulo a Chauta. Ngodala amene amasunga malamulo a Chauta, amene amafunafuna Chauta ndi mtima wao wonse, amene sachita zolakwa, koma amayenda m'njira za Chauta. Inu Chauta, mwapereka malamulo anu ndipo mwalamula kuti atsatidwe kwathunthu. Ndikadakonda kuti njira zanga zikhale zokhulupirika, pakumvera malamulo anu. Tsono anthu sadzandichititsa manyazi, ndikatsata malamulo anu onse. Ndidzakutamandani ndikuchita zoyenera, ndikaphunzira malangizo anu olungama. Ndidzatsata malamulo anu, musandisiye konse ndekha. Kodi mnyamata angathe bwanji kusunga makhalidwe ake kuti akhale angwiro? Akaŵasamala potsata mau anu. Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse, musalole kuti ndisiye kumvera malamulo anu. Ndasunga mau anu mumtima mwanga, kuti ndisakuchimwireni. Mutamandike, Inu Chauta, phunzitseni malamulo lanu. Ndimalalika ndi mau anga malangizo onse a pakamwa panu. Kuyenda m'njira ya malamulo anu kumandikondwetsa, kupambana kukhala ndi chuma chilichonse. Ndidzasinkhasinkha za malamulo anu, ndipo ndidzatsata njira zanu. Ndidzakondwera ndi malamulo anu, ndipo mau anu sindidzaŵaiŵala. Komereni mtima ine mtumiki wanu, kuti ndikhale ndi moyo ndi kusunga mau anu. Tsekulani maso anga kuti ndiwone zodabwitsa zochokera m'malamulo anu. Ndine munthu wongokhala nawo pa dziko lapansi, musandibisire malamulo anu. Mtima wanga wafooka chifukwa cholakalaka malangizo anu nthaŵi zonse. Inu mumadzudzula onyada, amene ali otembereredwa, amene amasiya malamulo anu. Mundichotsere zonyoza zao zondinyodola, chifukwa ndasunga malamulo anu. Ngakhale mafumu andichitire upo woipa, ine mtumiki wanu ndidzasinkhasinkhabe za malamulo anu. Malamulo anu amandikondwetsa, ndiwo amene amandilangiza. Ndangoti thapsa m'fumbi. Bwezereni moyo monga momwe mudalonjezera. Pamene ndidasimba za njira zanga, Inu mudandiyankha. Phunzitseni malamulo anu. Mundidziŵitse mfundo za malamulo anu, ndipo ndidzasinkhasinkha za ntchito zanu zodabwitsa. Ndafookeratu ndi chisoni. Limbitseni monga momwe mudalonjezera. Mundichotse m'njira zondisokeza, kuti ndisayendemo. Mundikomere mtima pondiphunzitsa malamulo anu. Ine ndasankhula njira yoti ndizikhala wokhulupirika, ndaika malangizo anu mumtima mwanga. Ndimakangamira malamulo anu, Inu Chauta, musalole kuti anthu andichititse manyazi. Ndidzatsata mokondwa njira ya malamulo anu, mukandiwonjezera nzeru. Chauta, phunzitseni njira zosungira malamulo anu, ndipo ndidzazitsata mpaka kumathero. Patseni nzeru kuti ndizisunga malamulo anu, ndiziŵatsata ndi mtima wanga wonse. Munditsogolere kuti ndimvere malamulo anu, chifukwa ndimakondwera nawo. Muphunzitse mtima wanga kuti uzikonda malamulo anu, osati chuma. Letsani maso anga kuti asamayang'ane zachabe, mundipatse moyo monga momwe mudalonjezera. Munditsimikizire ine mtumiki wanu chipangano chanu, chimene mumachita ndi anthu okuwopani. Mundichotsere chipongwe chimene ndimachiwopa, chifukwa malangizo anu ndi abwino. Onani ndikulakalaka kutsata malamulo anu. Mundipatse moyo chifukwa ndinu olungama. Chauta, mundikonde ndi chikondi chanu chosasinthika, mundipulumutse monga momwe mudalonjezera. Pamenepo ndidzakhala nchoŵayankha anthu ondinyodola, pakuti ndimakhulupirira mau anu. Pakamwa panga musapaletse mpang'ono pomwe kulankhula mau anu oona, pakuti ndimakhulupirira malangizo anu. Ndidzatsata malamulo anu kosalekeza mpaka muyaya, ndipo ndidzayenda ndi ufulu, chifukwa ndasamala malamulo anu. Ndidzalankhula malamulo anu pamaso pa mafumu, ndipo anthu sadzandichititsa manyazi. Inetu ndimasangalala ndi malamulo anu amene ndimaŵakonda. Ndimalemekeza malamulo anu amene ndimaŵakonda, ndipo ndimasinkhasinkha za malamulowo. Kumbukirani mau anu aja kwa ine mtumiki wanu, mau amene amandipatsa chikhulupiriro. Chimene chimandisangalatsa m'masautso anga nchakuti malonjezo anu amandipatsa moyo. Anthu osasamala za Mulungu amandinyoza kwathunthu, komabe sindisiyana nawo malamulo anu. Inu Chauta, ndikamalingalira malamulo anu akalekale, ndimasangalala, Ndimapsa mtima kwambiri chifukwa cha anthu oipa amene amaphwanya malamulo anu. Malamulo anu asanduka nyimbo yanga kulikonse kumene ndimapita. Ndimakukumbukirani usiku, Inu Chauta, ndipo ndimatsata malamulo anu. Madalitso ameneŵa andifikira ine, pakuti ndimatsata malamulo anu. Inu Chauta, zanga zonse ndinu, ndikulonjeza kumvera mau anu. Ndikukupemphani ndi mtima wanga wonse, mundikomere mtima molingana ndi malonjezo anu aja. Ndikamalingalira njira zanga, ndimatembenuka kuti nditsate malamulo anu. Ndimafulumira, sindizengereza kutsata malamulo anu. Ngakhale anthu oipa anditchere msampha, sindiiŵala malamulo anu. Ndimadzuka pakati pa usiku kuti ndikutamandeni, chifukwa cha malangizo anu olungama. Ine ndine bwenzi la anthu okuwopani, anthu otsata malamulo anu. Inu Chauta, dziko lapansi nlodzaza ndi chikondi chanu chosasinthika, phunzitseni malamulo anu. Inu Chauta, mwandikomera mtima mtumiki wanune, molingana ndi mau anu. Patseni luntha ndi nzeru, chifukwa ndimakhulupirira malamulo anu. Ndisanayambe kulangika ndinkasokera, koma tsopano ndimamvera mau anu. Inu ndinu abwino, ndipo mumachita zabwino, phunzitseni malamulo anu. Anthu osasamala za Mulungu amandisinjirira, komabe ndimatsata malamulo anu ndi mtima wanga wonse. Anthu otere ndi opulukira, koma ine ndimakondwa ndi malamulo anu. Ndi bwino kuti ndidalangidwa, kuti ndiphunzire malamulo anu. Malamulo a pakamwa panu amandikomera kuposa ndalama zikwizikwi zagolide ndi zasiliva. Manja anu adandilenga ndi kundiwumba. Patseni nzeru zomvetsa, kuti ndiziphunzira malamulo anu. Anthu okuwopani adzandiwona ndipo adzakondwa, popeza kuti ndakhulupirira mau anu. Inu Chauta, ndikudziŵa kuti kuweruza kwanu nkolungama, ndipo mwandilanga potsata kukhulupirika kwanu. Chikondi chanu chosasinthika chindisangalatse ine mtumiki wanu, monga momwe mudalonjezera. Mundichitire chifundo kuti ndikhale ndi moyo, pakuti malamulo anu amandikondwetsa. Anthu osasamala za Mulungu muŵachititse manyazi, chifukwa andilakwira pondinamizira. Koma ine ndidzasinkhasinkha za malamulo anu. Anthu okuwopani abwere kwa ine kuti aphunzire malamulo anu. Mtima wanga ukhale wopanda choudzudzulira pa malamulo anu, kuti ndisachite manyazi. Moyo wanga wafooka podikira chipulumutso chanu, ndikukhulupirira mau anu. Maso anga afiira nkuyang'anira malonjezo anu. Ndimafunsa kuti, “Kodi mudzandithandiza liti?” Ndasanduka ngati thumba lachikopa lokhwinyata, komabe sindiiŵala malamulo anu. Kodi mtumiki wanune ndipirire mpaka liti? Kodi anthu ondizunza mudzaŵalanga liti? Anthu osasamala za Mulungu, osatsata malamulo anu, andikumbira mbuna. Malamulo anu onse ndi osasinthika. Anthuwo amandizunza ndi mabodza ao; thandizeni! Adatsala pang'ono kundichotsa pa dziko lapansi, komabe sindidaleke kutsata malamulo anu. Sungani moyo wanga chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika, kuti nditsate malamulo anu. Inu Chauta, mau anu ngokhazikika kumwambako mpaka muyaya. Kukhulupirika kwanu kumakhala mpaka pa mibadwo yonse. Inu mwakhazikitsa dziko, ndipo siligwedezeka. Zolengedwa zikupezeka lero lino chifukwa cha kulamula kwanu, pakuti zinthu zonse zimakutumikirani. Malamulo anu akadapanda kundisangalatsa, bwenzi nditafa ndi mazunzo anga. Sindidzaiŵala konse malangizo anu, pakuti mwandipatsa nawo moyo. Ndine wanu, pulumutseni, pakuti ndasamala malamulo anu. Anthu oipa amandiŵenda kuti andiwononge, koma ine ndimalingalira za malamulo anu. Ndazindikira kuti zabwino zonse zili ndi malire, koma malamulo anu alibe konse malire. Ndimakonda malamulo anu kwambiri, ndimasinkhasinkha za malamulowo tsiku lonse. Malamulo anu amandisandutsa wanzeru kuposa adani anga, popeza kuti malamulowo ndili nawo nthaŵi zonse. Ndili ndi nzeru za kumvetsa kupambana aphunzitsi anga onse, pakuti ndimasinkhasinkha za malamulo anu. Ndili ndi nzeru kupambana okalamba, pakuti ndimatsata malamulo anu. Ndimaletsa miyendo yanga kuti isayende m'njira yoipa iliyonse, kuti choncho ndizisunga mau anu. Sindisiyana nawo malangizo anu, pakuti Inu mudandiphunzitsa mau anu ndi otsekemera kwambiri ndikaŵalaŵa. Amatsekemera kuposa uchi m'kamwa mwanga. Ndimakhala ndi nzeru za kumvetsa chifukwa cha malamulo anu. Nchifukwa chake ndimadana ndi njira iliyonse yonyenga. mau anu ndiye nyale ya mapazi anga, ndipo amaunikira njira yanga. Ndalumbirira, ndipo ndatsimikiza kuti ndidzamvera malangizo anu olungama. Ndazunzika koopsa, Chauta, patseni moyo, molingana ndi mau anu aja. Chauta, landirani mapemphero anga oyamika, ndipo mundiphunzitse malangizo anu. Moyo wanga uli m'zoopsa nthaŵi zonse, komabe sindiiŵala malamulo anu. Anthu oipa anditchera msampha, komabe sindisokera kuchoka m'njira ya malamulo anu. Malamulo anu ndiye madalitso anga mpaka muyaya, zoonadi, ndiwo amene amasangalatsa mtima wanga. Mtima wanga muuphunzitse kuti uzikonda malamulo anu nthaŵi zonse. Ndimadana nawo anthu apaŵiripaŵiri, koma ndimakonda mau anu. Inu ndinu malo anga obisalako ndiponso chishango changa, ndimakhulupirira mau anu. Chokereni inu, anthu ochita zoipanu, kuti ine ndizitsata malamulo a Mulungu wanga. Chirikizeni molingana ndi malonjezo anu aja, kuti ndizikhala ndi moyo, ndipo anthu asandichititse manyazi, chifukwa ndine wokhulupirika. Chirikizeni kuti ndipulumuke, kuti nthaŵi zonse ndizitsata malamulo anu. Inu mumaŵakana anthu onse osamvera malamulo anu, zoonadi, kuchenjera kwao nkopandapake. Anthu onse oipa a pa dziko lapansi, mumaŵayesa ngati zakudzala, nchifukwa chake ndimakonda malamulo anu. Thupi langa limanjenjemera chifukwa chokuwopani, ndimachita mantha ndi kuweruza kwanu. Ndachita zimene zili zolungama ndi zabwino. Musandisiye m'manja mwa ondizunza. Lonjezani kuti mudzandichitira zabwino mtumiki wanune, musalole anthu osasamala za Mulungu kuti andizunze. Maso anga atopa chifukwa cha kuyembekeza chipulumutso chanu, chifukwa cha kudikira kuti malonjezo anu olungama aja achitikedi. Komereni mtima mtumiki wanune, chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika, ndipo mundiphunzitse malamulo anu. Ndine mtumiki wanu, mundipatse nzeru zomvetsa, kuti ndizidziŵa malamulo anu. Yakwana nthaŵi yakuti Inu Chauta muchitepo kanthu, popeza kuti anthu aphwanya malamulo anu. Koma ine ndimasamala malamulo anu kupambana golide, golide wosungunula bwino. Malamulo anu onse amalungamitsa mayendedwe anga. Ndimadana ndi njira iliyonse yonyenga. Malamulo anu ndi abwino, nchifukwa chake ndimaŵatsata ndi mtima wanga wonse. Kufotokozera mau anu kumakhala ngati kuŵala, kumapatsa nzeru za kumvetsa kwa anthu opanda nzeru. Ndimapuma mwaŵefuŵefu nditatsekula pakamwa, chifukwa ndimalakalaka malamulo anu. Yang'aneni, ndipo mundikomere mtima monga m'mene mumachitira ndi anthu okukondani. Chirikizani mayendedwe anga molingana ndi mau anu aja, musalole kuti tchimo lililonse lizindilamulira. Pulumutseni kwa anthu ondizunza, kuti ndizitsata malamulo anu. Yang'anireni ine mtumiki wanu ndi chikondi chanu, ndipo mundiphunzitse malamulo anu. Maso anga akudza misozi yambiri ngati mitsinje, chifukwa anthu satsata malamulo anu. Ndinu olungama Chauta, ndipo kuweruza kwanu nkolungama. Malamulo amene mwatipatsa, ndi olungama ndi okhulupirika ndithu. Changu changa chikuyaka ngati moto mumtima mwanga, chifukwa adani anga amaiŵala mau anu. Malonjezo anu ndi otsimikizika, ndipo ine mtumiki wanu ndimaŵakonda. Ine ndine wamng'ono ndi wonyozeka, komabe sindiiŵala malamulo anu. Kulungama kwanu nkwamuyaya, ndipo malamulo anu ndi oona. Mavuto andigwera pamodzi ndi zoŵaŵa zomwe, koma malamulo anu amandisangalatsa. Malamulo anu ndi olungama mpaka muyaya, patseni nzeru zomvetsa kuti ndizikhala ndi moyo. Ndikulira kwa Inu ndi mtima wanga wonse, mundiyankhe, Inu Chauta. Ndidzatsata malamulo anu. Ndikukulirirani, mundipulumutse, kuti ndizitsata malamulo anu. Ndimadzuka tambala asanalire, kuti ndipemphe chithandizo. Ndimakhulupirira mau anu. Ndimakhala maso usiku wonse, ndikusinkhasinkha za malonjezo anu. Imvani liwu langa chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika. Inu Chauta, sungani moyo wanga chifukwa cha chilungamo chanu. Anthu ankhanza ondizunza akuyandikira. Iwo ali kutali ndi malamulo anu. Koma Inu Chauta muli pafupi, ndipo malamulo anu onse ndi oona. Poŵerenga malamulo anu ndidadziŵa kale lomwe kuti Inu mudaŵakhazikitsa mpaka muyaya. Yang'anani masautso anga, ndipo mundipulumutse, popeza kuti sindiiŵala malamulo anu. Munditchinjirize pa mlandu wanga, ndipo mundiwombole. Mundipatse moyo molingana ndi malonjezo anu aja. Chipulumutso chili kutali ndi anthu oipa, pakuti safunafuna malamulo anu. Chifundo chanu nchachikulu, Inu Chauta, mundipatse moyo molingana ndi chilungamo chanu. Anthu ondizunza ndiponso adani anga ngochuluka, koma sindisiyana nawo malamulo anu. Ndimanyansidwa ndikamayang'ana anthu osakhulupirika, chifukwa satsata malamulo anu. Onani m'mene ndimakondera malamulo anu, sungani moyo wanga chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika mau anu ndi oona okhaokha, malangizo anu onse olungama ngamuyaya. Mafumu amandizunza popanda chifukwa, koma mtima wanga umaopa mau anu. Ndimakondwa ndi mau anu monga munthu amene wapeza chuma chambiri. Ndimadana ndi anthu abodza, zoonadi, ndimanyansidwa nawo, koma ndimakonda malamulo anu. Ndimakutamandani kasanunkaŵiri pa tsiku, chifukwa cha malangizo anu olungama. Anthu okonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, palibe china chotha kuŵagwetsa. Ndimakhulupirira kuti mudzandipulumutsa, Inu Chauta, ndipo ndimatsata malamulo anu. Mzimu wanga umatsata malamulo anu, pakuti ndimaŵakonda ndi mtima wanga wonse. Ndimatsata malamulo anu ndi malangizo anu, pakuti makhalidwe anga onse mukuŵaona. Kulira kwanga kumveke kwa Inu, Chauta. Mundipatse nzeru zomvetsa potsata mau anu aja. Kupempha kwanga kumveke kwa Inu. Mundipulumutse potsata malonjezo anu. Pakamwa panga padzakutamandani, chifukwa mumandiphunzitsa malamulo anu. Ndidzaimba nyimbo zoyamikira mau anu, chifukwa malamulo anu onse ndi olungama. Dzanja lanu likhale lokonzeka kundithandiza, chifukwa ndatsata malamulo anu. Ndikulakalaka nthaŵi yoti mudzandipulumutse. Inu Chauta, malamulo anu amandikondwetsa. Lolani kuti ndikhale moyo, kuti ndizikutamandani, ndipo malangizo anu azindithandiza. Ndasokera ngati nkhosa yoloŵerera, koma mundifunefune ine mtumiki wanu, pakuti sindiiŵala malamulo anu. Nyimbo yoimba pokwera ku Yerusalemu. Ndimalirira Chauta m'mavuto anga kuti andiyankhe. Ndimati, “Pulumutseni, Inu Chauta, kwa anthu onama ndi kwa anthu onyenga.” Mulungu adzakuchitani chiyani, anthu onyenganu? Kodi adzakupatsani chilango cha mtundu wanji? Adzakuzunzani ndi mivi yakuthwa ya munthu wankhondo, pamodzi ndi makala amoto a mtengo wa tsanya. Ndili ndi tsoka lalikulu, chifukwa ndimakhala pakati pa anthu onga mbuli za ku Meseki ndi Kedara. Ndakhala nthaŵi yaitali pakati pa anthu odana ndi mtendere. Ine ndimafuna mtendere, koma ndikalankhula za mtendere, iwo amafuna nkhondo. Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti? Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi. Sadzalola phazi lako kuti literereke, Iye amene amakusunga sadzaodzera. Zoonadi, amene amasunga Israele, ndithu sadzaodzera kapena kugona. Chauta ndiye amene amakusunga, Chauta ndiye mtetezi wako ali ku dzanja lako lamanja. Dzuŵa silidzakupweteka masana, mwezi sudzakuvuta usiku. Chauta adzakuteteza ku zoipa zonse, adzasamala moyo wako. Chauta adzakusunga kulikonse kumene udzapita, kuyambira tsopano mpaka muyaya. Ndidasangalala pamene adandiwuza kuti, “Tiyeni tipite ku Nyumba ya Chauta.” Mapazi athu akhala akuima m'kati mwa zipata zako, iwe Yerusalemu. Yerusalemu adamangidwa bwino, zigawo zake zonse nzogwirizana pamodzi. Kumeneko kumapita mafuko onse, anthu ake a Chauta, monga momwe adalamulira Israele kuti akayamike dzina la Chauta. Kumeneko adaikako mipando yaufumu yoweruzira, mipando yake ya banja la Davide. Pemphererani mtendere wa Yerusalemu ponena kuti, “Anthu amene amakukonda iwe Yerusalemu, zinthu ziziŵayendera bwino. Mtendere ukhale m'kati mwa makoma ako, bata likhale m'nyumba zako zachifumu.” Chifukwa cha abale anga ndi abwenzi anga ndidzanena kuti, “Mtendere ukhaledi m'kati mwako.” Chifukwa cha Nyumba ya Chauta, Mulungu wathu, ndidzakupemphera zabwino. Ndikukweza maso anga kwa Inu, Inu amene mumakhala pa mpando wachifumu kumwamba. Monga momwe anyamata amayang'anira ku dzanja la bwana wao, monga momwe adzakazi amayang'anira ku dzanja la dona wao, ndi momwenso timayang'anira ife kwa Chauta Mulungu wathu, mpaka atatichitira chifundo. Mutichitire chifundo, Inu Chauta, mutichitire chifundo, pakuti adani athu atinyoza kopitirira malire. Pa nthaŵi yaitali, anthu olemera akhala akutinyodola, anthu onyada akhala akutinyoza. Chauta akadapanda kukhala pa mbali yathu, Israele anene choncho tsopano, Chauta akadapanda kukhala pa mbali yathu, pamene anthu adatiwukira, bwenzi atatimeza amoyo, muja mkwiyo wao udatiyakira, bwenzi chigumula chitatisesa, madzi amkokomo atatikokolola, bwenzi madzi amphamvu atatimiza. Atamandike Chauta, amene sadatipereke kwa anthuwo kuti atiwononge. Taonjoka ngati mbalame mu msampha wa osaka, msampha wathyoka, ndipo ife tapulumuka. Chithandizo chathu chimachokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi. Anthu amene amakhulupirira Chauta ndi olimba ngati phiri la Ziyoni, limene silingathe kugwedezeka, koma ndi lokhala mpaka muyaya. Monga momwe mapiri amazingira Yerusalemu, momwemonso Chauta akuzinga anthu ake kuyambira tsopano mpaka muyaya. Mafumu oipa sadzalamulira nthaŵi yonse dziko limene lapatsidwa kwa anthu ake, kuti nawonso anthu olungamawo angachite zoipa. Chauta, achitireni zabwino anthu amene ali abwino, amene ali olungama mtima. Koma anthu amene amatsata njira zao zokhotakhota, Chauta adzaŵapirikitsira kumene kuli anthu ochita zoipa. Mtendere ukhale ndi Israele. Pamene Chauta adabwezera akapolo ku Ziyoni, tinali ngati anthu amene akulota. Pamenepo tidasekera kwambiri, ndipo tidalulutira ndi chimwemwe. Tsono mitundu ina ya anthu inkanena kuti, “Chauta waŵachitira zazikulu.” Ndithudi, Chauta watichitira zazikulu, ndipo tasangalala. Tibwezereni ufulu wathu, Inu Chauta, tikhale ngati mitsinje yam'chipululu. Anthu amene amafesa akulira, adzakolola akufuula ndi chimwemwe. Munthu amene amapita akulira, atatenga mbeu zokafesa, adzabwerera kwao akufuula ndi chimwemwe, atatenga mitolo yake yambiri. Chauta akapanda kumanga nawo nyumba, omanga nyumbayo angogwira ntchito pachabe. Chauta akapanda kulonda nawo mzinda, mlonda angochezera pachabe. Mungodzivuta nkulaŵirira m'mamaŵa ndi kukagona mochedwa, kugwira ntchito movutikira kuti mupeze chakudya. Paja Chauta amapatsa okondedwa ake zosoŵa zao iwowo ali m'tulo. Zoonadi, ana ndi mphatso yochokera kwa Chauta, zidzukulu ndi mphotho yake. Ana apaunyamata ali ngati mivi m'manja mwa munthu wankhondo. Ngwodala amene phodo lake nlodzaza ndi mivi yotere. Sadzamchititsa manyazi akamalankhula ndi adani ake pa bwalo lamilandu. Ngwodala aliyense woopa Chauta, amene amayenda m'njira zake. Udzadya zimene manja ako adagwirira ntchito. Udzasangalala, ndipo zinthu zidzakuyendera bwino. Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka, m'kati mwa nyuma yako. Ana ako adzakhala ngati tiziphukira taolivi, kuzungulira tebulo lako. Zoonadi, ndimo m'mene adzakhalire wodala munthu woopa Chauta. Chauta amene amakhala ku Ziyoni akudalitse. Uwone m'mene Yerusalemu zinthu zidzamuyendere bwino masiku onse a moyo wako. Ukhale ndi moyo wautali kuti uwone zidzukulu zako. Mtendere ukhale ndi Israele. “Adani akhala akundizunza kwambiri kuyambira unyamata wanga,” Israele anene choncho tsopano, “Adani akhala akundizunza kwambiri kuyambira unyamata wanga, komabe sadandipambane. “Pondikwapula adani anga adachita ngati kulima pamsana panga, kulima mizere yaitali.” Koma Chauta ndi wolungama, wandimasula zingwe za anthu oipa. Anthu onse odana ndi Ziyoni agonjetsedwe ndi kupirikitsidwa mwamanyazi. Akhale ngati udzu womera pa denga la nyumba, umene umafota usanakule. Woumweta sangadzaze nkumanja komwe, womanga mitolo sangamange nchitsakato chomwe. Anthu odutsapo sadzanena kwa omwetawo kuti, “Madalitso a Chauta akhale nanu.” “Tikukudalitsani potchula dzina la Chauta.” Ndikulirira Inu Chauta, ndili m'dzenje lozama lamavuto. Ambuye imvani liwu langa. Tcherani khutu kuti mumve kupemba kwanga. Inu Chauta, mukadaŵerengera machimo, ndani akadakhala chilili opanda mlandu, Ambuye? Koma inu mumakhululukira, nchifukwa chake timakulemekezani. Ndimayembekeza chithandizo cha Chauta, ndimayembekeza ndi mtima wonse, ndipo ndimakhulupirira mau ake. Mtima wanga umayembekeza Chauta kupambana m'mene alonda amayembekezera mbandakucha, kupambanadi m'mene alonda amayembekezera mbandakucha. Iwe Israele, khulupirira Chauta. Paja Chauta ndi wa chikondi chosasinthika, ndi wokonzeka kupulumutsa. Adzaombola Israele ku machimo ake onse. Chauta, mtima wanga ndi wosadzikuza, maso anga ndi osanyada. Sinditengeka mtima ndi zinthu zapamwamba ndi zodabwitsa. Koma ndautonthoza ndi kuukhalitsa chete mtima wanga, monga mwana amene mai wake amamtonthoza ndi bere. Momwemo mtima wanga uli phe m'kati mwanga. Iwe Israele, khulupirira Chauta kuyambira tsopano mpaka muyaya. Inu Chauta, mukumbukire Davide ndi mavuto onse amene adaŵapirira. Adalumbira kwa Inu Chauta, nalonjeza kwa Mulungu Wamphamvuzonse wa Yakobe kuti, “Ndithu sindidzaloŵa m'nyumba mwanga, kapena kukagona pabedi panga, sindidzalola kuti ndikhale m'tulo kapena kuti zikope zanga ziwodzere, mpaka nditapezera Chauta malo, malo oti Mulungu Wamphamvuzonse wa Yakobe azikhalamo.” Tidamva za bokosi lachipangano ku Efurata, tidalipeza m'minda ya ku Yaara. “Tiyeni tipite kumalo kumene Chauta amakhala. Tiyeni tikapembedze ku mpando wake wachifumu.” Dzambatukani, Inu Chauta, ndi kupita ku malo anu kumene mumakhala, Inuyo pamodzi ndi bokosi lachipangano lofanizira mphamvu zanu. Ansembe anu avale chilungamo ngati nsalu, anthu anu oyera mtima afuule ndi chimwemwe. Chifukwa cha zimene mudalonjeza kwa mtumiki wanu Davide, musakane nkhope ya wodzozedwa wanu. Chauta adalumbirira Davide momtsimikizira, ndipo sadzasintha, adati, “Ndidzakhazika pa mpando wachifumu mmodzi mwa ana ako aamuna. Ngati ana ako aamuna asunga chipangano changa ndi malamulo anga amene ndidzaŵaphunzitsa, ana aonso adzakhala pa mpando wako wachifumu mpaka muyaya.” Chauta wasankhula Ziyoni, akufuna kuti akhale malo ake okhalamo. Akuti, “Ameneŵa ndiwo malo anga opumuliramo mpaka muyaya. Ndidzakhala kuno chifukwa ndakufunitsitsa. “Ndidzadalitsa kwambiri mzinda wa Ziyoni poupatsa zosoŵa zake, anthu ake osauka, ndidzaŵapatsa chakudya chokwanira. Ansembe ake ndidzaŵaveka chipulumutso, anthu ake oyera mtima adzafuula ndi chimwemwe. “Davide ndidzammeretsera chiphukira kumeneko. Ndamkonzera nyale wodzozedwa wanga. Adani ake ndidzaŵaveka manyazi ngati nsalu, koma iye yekhayo adzavala chisoti choŵala chachifumu.” Ati kukoma ndi kukondweretsa ati, anthu akakhala amodzi mwaubale! Ndi ngati mafuta amtengowapatali oŵathira pa mutu, otsikira ku ndevu, ku ndevu za Aroni, oyenderera mpaka ku khosi la mkanjo wake. Ndi ngati mame a ku Heremoni, omatsikira ku mapiri a Ziyoni. Ku Ziyoni Chauta amaperekako madalitso, ndiye kuti moyo wamuyaya. Bwerani, mudzatamande Chauta, Inu nonse atumiki a Chauta, inu amene mumatumikira m'Nyumba mwake usiku. Kwezani manja anu popemphera m'malo ake oyera, ndipo mutamande Chauta. Akudalitseni Chauta amene amakhala ku Ziyoni, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi. Tamandani Chauta. Tamandani dzina la Chauta, Perekani matamando, inu atumiki a Chauta, inu amene mumatumikira m'Nyumba ya Chauta, m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu wathu! Tamandani Chauta, pakuti ngwabwino. Muimbireni nyimbo zotamanda dzina lake, pakuti nlokoma kwambiri. Wadzisankhulira Yakobe kuti akhale wake, Israele kuti akhale chuma chake. Pakuti ndimadziŵa kuti Chauta ndi wamkulu, kuti Chauta, Mulungu wathu, ndi wamphamvu kupambana milungu yonse. Chilichonse chimene Chauta amafuna kuchita amachitadi kumwamba ndi pa dziko lapansi, m'nyanja ndi monse mozama. Ndiye amene amatulutsa mitambo ku mathero a dziko lapansi, amene amachititsa zing'aning'ani za mvula, amene amaombetsa mphepo kuchokera m'nkhokwe zake. Ndiye amene adapha ana achisamba a ku Ejipito, ana a anthu ndi a nyama omwe, amene adaonetsa Farao ndi atumiki ake onse zizindikiro zamphamvu ndi zodabwitsa m'dziko la Ejipito. Ndiye amene adaononga mitundu yambiri ya anthu, ndi kupha mafumu amphamvu aja, Sihoni, mfumu ya Aamori, ndi Ogi, mfumu ya ku Basani, pamodzi ndi maufumu onse a ku Kanani. Adapereka dziko lao kuti likhale choloŵa, choloŵa cha Aisraele, anthu ake. Dzina lanu, Inu Chauta, nlamuyaya, kutchuka kwanu ndi kwa pa mibadwo yonse. Pakuti Chauta adzaweruza anthu ake kuti alibe mlandu, adzachitira chifundo atumiki ake. Mafano a mitundu ina ya anthu ndi asiliva ndi agolide chabe, ndi opangidwa ndi manja a anthu. Pakamwa ali napo, koma salankhula, maso ali nawo, koma sapenya. Makutu ali nawo, koma saamva, ndipo alibe mpweya m'kamwa mwao. Anthu amene amapanga mafanowo afanefane nawo, chimodzimodzi onse amene amaŵakhulupirira. Inu a m'banja la Israele, tamandani Chauta! Inu a m'banja la Aroni, tamandani Chauta! Inu a banja la Levi, tamandani Chauta! Inu amene mumaopa Chauta, tamandani Chauta! Atamandike ku Ziyoni Chauta, amene amakhala ku Yerusalemu! Tamandani Chauta! hokozani Chauta chifukwa ngwabwino, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Thokozani Mulungu wa milungu, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Thokozani Chauta woposa ambuye onse, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Chauta yekhayo amachita zodabwitsa zazikulu, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Adalenga zakumwamba ndi nzeru zake, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Adayala dziko lapansi pa madzi, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Adalenga miyuni yaikulu yamumlengalenga, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Dzuŵa kuti lizilamulira usana, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Mwezi ndi nyenyezi kuti zizilamulira usiku, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Adapha ana achisamba a ku Ejipito, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Ndipo adatulutsa Aisraele pakati pao, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambalitsa, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Adagaŵa pakati Nyanja Yofiira, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Adaolotsa Aisraele pakati pake, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Koma adamiza Farao ndi ankhondo ake m'Nyanja Yofiira, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Adatsogolera anthu ake m'chipululu, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Adapha mafumu amphamvu, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Adaphanso mafumu otchuka, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Adapha Sihoni, mfumu ya Aamori, pakuti chikondi chake nchamuyaya, Adapha Ogi, mfumu ya ku Basani, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Napereka dziko la mafumuwo kuti likhale choloŵa, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Choloŵa cha Israele mtumiki wake, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Adatikumbukira pamene adani adatigonjetsa, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Ndipo adatipulumutsa kwa adani athu, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Amapatsa zamoyo zonse chakudya, pakuti chikondi chake nchamuyaya. Thokozani Mulungu wakumwamba, pakuti chikondi chake nchamuyaya. M'mbali mwa mitsinje ya ku Babiloni, kumeneko tidakhala pansi nkumalira tikukumbukira Ziyoni. Kumeneko tidapachika apangwe athu pa mitengo ya misondodzi. Kumeneko anthu otigwira ukapolo adatipempha kuti tiimbe nyimbo. Otizunza adatipempha kuti tisangalale, adati, “Tatiimbiraniko nyimbo ya ku Ziyoni.” Tsono ife tidati, “Tingaimbe bwanji nyimbo ya Chauta kuchilendo ngati kuno?” Ndikakuiŵala iwe Yerusalemu, dzanja langa lamanja liwume. Lilime langa likangamire ku mnakanaka m'kamwa mwanga, ndikapanda kukukumbukira iwe Yerusalemu ndi kukuwona kuti ndiwe wondisangalatsa kwambiri. Kumbukirani, Inu Chauta, zimene adachita Aedomu pa tsiku lija la kuwonongeka kwa Yerusalemu, muja ankati, “Mgwetseni pansi, mgwetseni pansi, mpaka pa maziko ake.” Mzinda wa Babiloni, iwe woyenera kuwonongedwawe, adzakhala wodala munthu amene adzakubwezera zimene watichita ifezi. Adzakhala wodala munthu amene adzatenga makanda ako ndi kuŵakankhanthitsa ku thanthwe. Ndikukuthokozani Inu Chauta ndi mtima wanga wonse. Ndikuimba nyimbo zokutamandani pamaso pa milungu. Ndikugwada moŵerama kumaso kwa Nyumba yanu yoyera. Ndikutamanda dzina lanu chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika, chifukwanso cha kukhulupirika kwanu. Mwakweza dzina lanu ndiponso malonjezo anu kupambana chinthu china chilichonse. Pa tsiku limene ndidakuitanani, Inu mudandiyankha, mumandilimbitsa mtima ndi mphamvu zanu. Mafumu onse a m'dziko adzakutamandani, Inu Chauta, chifukwa amva mau a pakamwa panu. Adzaimba nyimbo zotamanda njira za Chauta, pakuti ulemerero wa Chauta ndi waukulu. Ngakhale Chauta ndi wamphamvu, amasamalira anthu otsika, koma anthu odzikuza amaŵadziŵira chapatali. Ngakhale ndiyende pakati pa mavuto, Inu mumasunga moyo wanga. Mumatambasula dzanja lanu kuletsa adani anga okwiya, dzanja lanu lamanja limandipulumutsa. Chauta adzaona kuti cholinga chake pa ine chichitikedi. Chikondi chanu, Inu Chauta, nchamuyaya. Muipitirize ntchito imene mwaiyambayo. Chauta mwafufuzafufuza, ndipo mwandidziŵa. Inu mumadziŵa pamene ndikhala pansi, pamenenso ndidzuka, mumazindikira maganizo anga muli kutali. Mumandipenyetsetsa ndikamayenda ndiponso ndikamagona, mumadziŵa njira zanga zonse. Ngakhale mau anga asanafike pakamwa panga, Inu Chauta mumaŵadziŵa onse. Mumandizinga kumbuyo ndi kutsogolo, ndipo mumandisanjika dzanja lanu. Nzeru zimenezi nzopitirira nzeru zanga, nzapamwamba, sindingathe kuzimvetsa. Ndidzapita kuti, pofuna kupewa Mzimu wanu, kapena pofuna kuthaŵa nkhope yanu? Ndikakwera kumwamba, Inu muli komweko, ndikagona m'dziko la anthu akufa, Inu muli momwemo. Ndikaulukira kotulukira dzuŵa, kapena kukafika kuzambwe, ku mathero a nyanja, ngakhale kumenekonso mudzanditsogolera, dzanja lanu lamanja lidzandichirikiza. Ndikanena kuti, “Mdima undiphimbe, kuŵala kumene kwandizinga kusanduke mdima,” ngakhale mdimawo, kwa Inu si mdima konse, kwa Inu usiku umaŵala ngati usana, mdima uli ngati kuŵala. Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri. Mapangidwe anga sadabisike pamaso panu pamene ndinkapangidwa mwachinsinsi, pamene ndinkaumbidwa mwaluso m'mimba mwa amai anga. Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe. Maganizo anu, Inu Mulungu, ndi ozama kwa ine, ndi osaŵerengeka konse. Ndikadaŵaŵerenga, bwenzi ali ambiri koposa mchenga. Ndikamadzuka ndimakhala nanube. Ndikadakonda kuti muwononge anthu oipa, Inu Mulungu, ndipo kuti anthu okhetsa magazi andichokere. Anthuwo amakunenani zinthu zoipa, namakuukirani ndi mtima woipa. Kodi sindidana nawo anthu odana nanu, Inu Chauta? Kodi sindinyansidwa nawo anthu okuukirani? Ndimadana nawo ndi chidani chenicheni. Ndimaŵayesa adani anga. Fufuzeni, Inu Mulungu, kuti mudziŵe mtima wanga. Yeseni kuti mudziŵe maganizo anga. Muwone ngati ndimatsata njira yoipa iliyonse, ndipo munditsogolere m'njira yanu yamuyaya. Pulumutseni, Inu Chauta, kwa anthu oipa. Tchinjirizeni kwa anthu ankhanza. Iwo amalingalira mumtima mwao kuti achite zoipa, amautsa nkhondo nthaŵi zonse. Amanola lilime lao kuti likhale ngati la njoka, m'kamwa mwao muli ululu wa mamba. Inu Chauta, tetezeni kwa anthu oipa, tchinjirizeni kwa anthu andeu, amene amaganiza zofuna kundigwetsa. Anthu odzikuza anditchera msampha mobisika, atchera ukonde wa zingwe, anditchera misampha m'mbali mwa njira. Ndimauza Chauta kuti, “Inu ndinu Mulungu wanga,” tcherani khutu kuti mumve liwu la kupemba kwanga, Inu Chauta. Inu Chauta, Ambuye anga, Mpulumutsi wanga wamphamvu, mwateteza moyo wanga pa tsiku lankhondo. Inu Chauta, musampatse munthu woipa zokhumba zake. Musathandizire chiwembu chake. Adani anga ondizinga asandigonjetse. Mau ao otemberera aŵabwerere. Makala amoto aŵagwere, aponyedwe m'maenje ozama, asatulukemonso. Musalole kuti woononga mbiri ya mnzake akhazikike m'dziko. Choipa chimlondole munthu wankhanza mpaka kumuwononga. Ndimadziŵa kuti Inu Chauta mumateteza ozunzika, mumaweruza mwachilungamo anthu osoŵa. Zoonadi, anthu ochita zabwino adzatamanda dzina lanu. Anthu amenewo adzakhala pamaso panu. Ndikukuitanani, Inu Chauta, fulumirani kudzandithandiza. Tcherani khutu kuti mumve liwu langa pamene ndikupemphera kwa Inu. Pemphero langa likwere kwa Inu ngati lubani, kukweza kwa manja anga kukhale ngati nsembe yamadzulo. Muike mlonda pakamwa panga, Inu Chauta. Mulonde pa khomo la milomo yanga. Musalole kuti mtima wanga upendekere ku zoipa, ndisadzipereke ku ntchito zoipa pamodzi ndi anthu ochita zoipa, ndisadye nawo maphwando ao. Munthu wolungama angathe kundimenya kapena kundidzudzula chifukwa andimvera chifundo, koma ndisalandire ulemu kwa anthu oipa, pakuti ndimapemphera motsutsana ndi ntchito zao zoipa. Anthu oipa akadzaperekedwa kwa oŵalanga, pamenepo adzaphunzira kuti mau a Chauta ndi oona. Monga momwe nkhuni zimamwazikira akaziŵaza, ndi m'menenso mafupa ao adzamwazikira ku manda. Koma maso anga amayang'anirabe kwa Inu, Chauta Mulungu wanga. Ndimathaŵira kwa Inu kuti munditeteze, musandisiye opanda wonditchinjiriza. Mundipulumutse ku msampha umene iwo anditchera, ndi ku makhwekhwe a anthu ochita zoipa. Anthu oipa akodwe pamodzi mu ukonde wao womwe, koma ine ndipulumuke. Ndikulirira Chauta mokweza, ndikupemba kwa Chauta mofuula. Ndikupereka madandaulo anga kwa Iye, ndikutchula mavuto anga pamaso pake. Pamene mtima wanga ufooka, Inu mumadziŵa zoti ndichite. Adani anditchera msampha m'njira imene ndimayendamo. Ndikayang'ana ku dzanja lamanja, palibe ndi mmodzi yemwe wosamalako za ine. Kulibe koti ndithaŵire, palibe munthu wondisamala. Ndimalirira Inu Chauta, ndimati, “Inu ndinu kothaŵira kwanga, ndinu zanga zonse m'dziko la amoyo.” Imvani kulira kwanga, pakuti ndataya mtima. Pulumutseni kwa ondizunza, chifukwa andiposa mphamvu. Tulutseni m'ndende kuti ndizitamanda dzina lanu. Anthu anu adzandizungulira, chifukwa Inu mwandichitira zabwino zambiri. Imvani pemphero langa, Inu Chauta. Tcherani khutu kuti mumve kupemba kwanga. Mundiyankhe chifukwa cha kukhulupirika kwanu ndi kulungama kwanu. Musandizenge mlandu ine mtumiki wanu, popeza kuti palibe munthu wamoyo amene ali wolungama pamaso panu. Mdani wandilondola, wavimviniza moyo wanga m'dothi, wandikhazika mu mdima, ngati anthu amene adafa kale. Nchifukwa chake mtima wanga wafooka m'kati mwanga, mumtima mwangamu mukuchita mantha. Ndimakumbukira masiku amakedzana, ndimasinkhasinkha za zonse zimene mwazichita, ndimalingalira ntchito za manja anu. Ndimatambalitsira manja anga kwa Inu, mtima wanga umamva ludzu lofuna Inu, monga limachitira dziko louma. Fulumirani kundiyankha, Inu Chauta. Ndataya mtima kwambiri, musandibisire nkhope yanu, kuti ndingafanefane ndi anthu otsikira ku manda. Lolani kuti m'maŵa ndimve za chikondi chanu chosasinthika, chifukwa ndimakhulupirira Inu. Mundisonyeze njira yoti ndiziyendamo, pakuti ndimapereka mtima wanga kwa Inu. Inu Chauta, pulumutseni kwa adani anga, chifukwa ndathaŵira kwa Inu. Phunzitseni, kuti ndizichita zofuna Inu, pakuti ndinu Mulungu wanga. Mzimu wanu wabwino unditsogolere pa njira yanu yosalala. Sungani moyo wanga, Inu Chauta, kuti dzina lanu lilemekezeke. Munditulutse pa mavuto chifukwa cha kulungama kwanu. Kanthani adani anga chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika pa ine. Muwononge onse ondizunza, pakuti ine ndine mtumiki wanu. Atamandike Chauta, thanthwe langa londitchinjiriza, amene amaphunzitsa manja anga ndi zala zanga kumenya nkhondo. Ndiye thanthwe langa ndi tchemba langa londiteteza, ndiye linga langa londipulumutsa, ndiye chishango changa chothaŵirako. Amaika mitundu ya anthu mu ulamuliro wanga. Inu Chauta, kodi munthu nchiyani, kuti muzimsamala? Mwana wa munthu nchiyani, kuti muzimganizira? Munthu ali ngati mpweya, masiku ake ali ngati mthunzi wosakhalitsa. Ng'ambani thambo, Inu Chauta, ndi kutsikira pansi. Khudzani mapiri kuti afuke nthunzi. Ng'animitsani zing'aning'ani ndi kuŵamwaza adani anga. Ponyani mivi yanu, ndi kuŵapirikitsa. Tambasulani dzanja lanu kuchokera kumwamba. Landitseni ndi kundipulumutsa ku madzi ozama, omboleni m'manja mwa akunja, amene amalankhula zabodza, ndipo amalumbira zonama. Ndidzakuimbirani nyimbo yatsopano, Inu Mulungu. Ndidzakuimbirani zeze wa nsambo khumi, Inu amene mumapambanitsa mafumu pankhondo, amene mumalanditsa Davide mtumiki wanu. Landitseni kwa adani ankhalwe, mundipulumutse m'manja mwa akunja, amene amalankhula zabodza, ndipo amalumbira zonama. Ana athu aamuna pachinyamata pao akhale amphamvu ngati mitengo, ana athu aakazi akhale okongola ngati nsanamira zozokotedwa zapangodya, zoti zikometse nyumba yaufumu. Nkhokwe zathu zikhale zodzaza, zisunge zokolola za mtundu uliwonse. Nkhosa zathu zibale ana zikwizikwi m'mabusa athu. Ng'ombe zathu zikhale ndi maŵele, zisapoloze kapena kulephera kubereka. M'miseu mwathu musakhale kulira chifukwa cha mavuto. Ngodala anthu olandira madalitso ameneŵa. Ngodala anthu amene Mulungu wao ndi Chauta. Ndidzakuyamikani, Inu Mulungu wanga, mfumu yanga, ndidzalemekeza dzina lanu nthaŵi zonse mpaka muyaya. Ndidzakuthokozani tsiku ndi tsiku, ndidzatamanda dzina lanu mpaka muyaya. Chauta ndi wamkulu ndi woyenera kumtamanda kwambiri, ndipo ukulu wake sitingathe kuumvetsa. Mibadwo ndi mibadwo idzatamanda ntchito zanu, idzalalika ntchito zanu zamphamvu. Ndidzasinkhasinkha za ulemerero ndi za ufumu wanu waukulu, ndidzalingalira za ntchito zanu zodabwitsa. Anthu adzasimba za mphamvu zanu zoopsa, inenso ndidzalalika za ukulu wanu. Adzasimba za ubwino wanu, adzaimba nyimbo zotamanda kulungama kwanu. Chauta ndi wokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika. Chauta ndi wabwino kwa onse, amachitira chifundo zamoyo zonse zimene adazilenga. Zamoyo zonse zidzakuthokozani, Inu Chauta, anthu anu onse oyera mtima adzakutamandani. Adzalankhula za ulemerero wa ufumu wanu, adzasimba za mphamvu zanu, kuti adziŵitse anthu onse za ntchito zanu zamphamvu, kutinso asimbe za ulemerero ndi za ufumu wanu waukulu. Ufumu wanu ndi ufumu wamuyaya, ulamuliro wanu ndi wa pa mibadwo yonse. Chauta ndi wokhulupirika pa mau ake onse, ndi wokoma mtima pa zochita zake zonse. Chauta amachirikiza onse ogwa m'mavuto, amakweza onse otsitsidwa. Maso onse amayang'anira kwa Inu, ndipo mumaŵapatsa chakudya pa nthaŵi yake. Mumafumbatula dzanja lanu, ndipo mumapatsa chamoyo chilichonse zofuna zake. Chauta ndi wolungama m'zochita zake zonse, ndi wachifundo pa zonse zimene achita. Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika. Amene amamvera Chauta, amaŵapatsa zofuna zao, amamvanso kulira kwao, naŵapulumutsa. Onse amene amakonda Chauta, amaŵasunga, koma Chauta adzaononga oipa onse. Pakamwa panga padzayamika Chauta, zamoyo zonse zitamande dzina lake loyera mpaka muyaya. Tamandani Chauta! Tamanda Chauta, iwe mtima wanga. Ndidzatamanda Chauta pa moyo wanga wonse. Ndidzaimba nyimbo zotamanda Mulungu wanga nthaŵi zonse pamene ndili moyo. Musakhulupirire mafumu kapena anthu ena amene sangathe kuthandiza. Pamene mpweya wa munthu uchokeratu, munthuyo amabwerera ku dothi, zimene ankafuna kuchita, zimatha tsiku lomwelo. Ngwodala munthu amene chithandizo chake chimafumira kwa Mulungu wa Yakobe, munthu amene amakhulupirira Chauta, Mulungu wake. Chauta adalenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili m'menemo. Amasunga malonjezo ake nthaŵi zonse. Amachitira anthu opsinjidwa zolungama, amaŵapatsa chakudya anthu anjala. Chauta amamasula am'ndende. Chauta amatsekula maso a anthu osapenya, Chauta amakweza anthu otsitsidwa. Chauta amakonda anthu ochita chilungamo. Chauta amateteza alendo, amachirikiza mkazi wamasiye ndiponso mwana wamasiye. Koma njira za anthu oipa amazipotoza. Chauta adzakhala mfumu mpaka muyaya, Mulungu wako, iwe Ziyoni, adzalamulira ku mibadwo yonse. Tamandani Chauta! Tamandani Chauta! Nkwabwino kuimba nyimbo zotamanda Mulungu wathu, nkokondwetsa mtima kumtamanda moyenera. Chauta akumanga Yerusalemu, akusonkhanitsa Aisraele omwazika. Akuchiritsa a mtima wachisoni, ndipo akumanga mabala ao. Amadziŵa chiŵerengero cha nyenyezi, zonse amazitcha maina ake. Mbuye wathu ndi wamkulu, ndipo ndi wa mphamvu zambiri, nzeru zake nzopanda malire. Amakweza oponderezedwa, koma amagwetsa pansi anthu oipa. Imbirani Chauta mothokoza, imbirani Mulungu wathu nyimbo yokoma ndi pangwe. Amaphimba zakumwamba ndi mitambo, amapatsa nthaka mvula, amameretsa udzu pa magomo. Amapereka chakudya kwa nyama ndi kwa ana a khungubwi pamene akulira chakudya. Mphamvu za kavalo saziyesa kanthu, mphamvu za ankhondo sazisamala. Koma Chauta amakondwera ndi anthu omuwopa, amene amadalira chikondi chake chosasinthika. Tamanda Chauta, iwe Yerusalemu. Tamanda Mulungu wako, iwe Ziyoni. Paja amalimbitsa mipiringidzo ya zipata zako. Amadalitsa anthu amene ali mwa iwe. Amadzetsa mtendere m'malire a dziko lako, amakudyetsa pokupatsa ufa wa tirigu wosalala. Akapereka lamulo pa dziko lapansi, mau ake amayenda mwaliŵiro. Amagwetsa chisanu chambee ngati ubweya. Amamwaza chipale ngati phulusa. Amagwetsa matalala ngati miyala. Kodi ndani angathe kupirira kuzizira kwake? Akalamula kuti zichoke, pomwepo zimasungunuka, akaombetsa mphepo, madzi amayenda. Amadziŵitsa Yakobe mau ake, amaphunzitsa Israele malamulo ake ndi malangizo ake. Sadachitepo zimenezi ndi mtundu wina uliwonse wa anthu, iwo sadziŵa malangizo ake. Tamandani Chauta! Tamandani Chauta! Tamandani Chauta inu okhala kumwamba, mtamandeni inu okhala mu mlengalenga! Mtamandeni inu angelo ake onse, mtamandeni inu magulu a ankhondo ake onse! Mtamandeni inu dzuŵa ndi mwezi, mtamandeni inu nonse nyenyezi zoŵala! Mtamandeni inu thambo lakumwambamwamba, ndi inu madzi a pamwamba pa thambo! Zonsezo zitamande dzina la Chauta! Paja Iye adaalamula, izo nkulengedwa. Adazikhazikitsa kuti zikhale mpaka muyaya, adaikapo lamulo limene silingathe kusinthika. Tamandani Chauta inu okhala pa dziko lapansi, inu zilombo za m'madzi ndi nyanja zonse zozama, inu moto ndi matalala, inu chisanu chambee ndi mitambo, inu mphepo zamkuntho, okwaniritsa zolamula Chauta! Inu mapiri onse ndi zitunda zonse, inu mitengo yazipatso ndi mikungudza yonse! Inu nyama zakutchire ndi zoŵeta zonse, inu zinthu zokwaŵa ndi mbalame zouluka! Inu mafumu a pa dziko lapansi ndi anthu a mitundu yonse, inu akuluakulu ndi olamulira dziko lapansi! Inu anyamata pamodzi ndi anamwali, inu nkhalamba ndi ana omwe! Onsewo atamande dzina la Chauta, pakuti dzina lake lokha nlolemekezeka, ulemerero wake ndi woposa, pansi pano nkumwamba komwe. Chauta wakweza anthu ake poŵapatsa mphamvu. Walemekeza anthu ake onse oyera mtima, Aisraele amene Iye amaŵakonda. Tamandani Chauta! Tamandani Chauta! Imbirani Chauta nyimbo yatsopano, imbani nyimbo yomtamanda pa msonkhano wa anthu ake oyera mtima. Aisraele asangalale ndi Mlengi wao. Anthu a Ziyoni akondwere ndi Mfumu yao. Atamande dzina lake povina, amuimbire nyimbo yokoma ndi ng'oma ndi pangwe. Paja Chauta amakondwera ndi anthu ake, amaŵalemekeza anthu odzichepetsa poŵagonjetsera adani ao. Okhulupirika akondwerere chigonjetso chopambanachi, aziimba mokondwa ali gone pa mabedi. Atamande Mulungu kwambiri mokweza mau, malupanga akuthwa konsekonse ali m'manja, kuti alipsire mafuko achikunja, kuti alange mitundu ina ya anthu. Amange mafumu ao ndi maunyolo, amange atsogoleri ao ndi zitsulo, kuti aŵalange monga momwe Mulungu adalamulira. Umenewu ndiwo ulemerero wa anthu okhulupirira Chauta. Tamandani Chauta! Tamandani Chauta! Tamandani Mulungu m'malo ake opatulika. Mtamandeni ku thambo lake lamphamvu. Mtamandeni chifukwa cha ntchito zake zamphamvu, mtamandeni chifukwa cha ukulu wake wopambana. Mtamandeni pomuimbira lipenga, mtamandeni ndi gitara ndi zeze. Mtamandeni poimba ng'oma ndi povina, mtamandeni ndi zipangizo zansambo ndi mngoli. Mtamandeni ndi ziwaya zamalipenga zolira, mtamandeni ndi ziwaya zamalipenga zolira kwambiri. Chamoyo chilichonse chopuma chitamande Chauta. Tamandani Chauta! Aŵa ndi malangizo a Solomoni, mwana wa Davide, mfumu ya Israele. Ngothandiza kuti anthu adziŵe nzeru ndi mwambo, kuti amvetse mau a matanthauzo ozama, kuti alandire mwambo wochita zinthu mwanzeru, akhale angwiro, achilungamo ndi osakondera. Ngophunzitsa anthu wamba nzeru za kuchenjera, ndi achinyamata kudziŵa zinthu ndi kulingalira bwino. Ndi oti wanzeru akaŵamva, aonjezere kuphunzira kwake, ndipo munthu womvetsa zinthu apate luso, kuti azimvetsa miyambi ndi mafanizo, mau a anthu anzeru ndi mikuluŵiko yao. Kuwopa Chauta ndiye chiyambi cha nzeru. Zitsiru ndiye zimanyoza nzeru ndi malangizo. Mwana wanga, umvere zimene bambo wako akukulangiza, usakane zimene mai wako akukuphunzitsa. Zili ngati nsangamutu yokongola yamaluŵa pamutu pako, zili ngati mkanda wa m'khosi mwako. Mwana wanga, anthu oipa akafuna kukukopa, usamaŵamvera. Adzati, “Tiye kuno, tikabisale kuti tiphe anthu, tiye tikalalire anthu osalakwa. Tiyeni tiŵameze amoyo ngati manda, tiŵameze athunthu ngati anthu otsikira ku manda. Motero tidzapata zinthu zambiri zamtengowapatali, nyumba zathu tidzazidzaza ndi zofunkha. Tiye uloŵe m'gulu lathu, chuma chathu tidzagaŵana tonse.” Mwana wanga, usamayenda nawo anthu amenewo, usatsagane nawo pa njira yaoyo. Paja iwowo amangofuna zoipa zokhazokha, amathamangira kupha basi. Nkopanda phindu kutchera kumwezi, nanga mbalame siziwona! Koma anthu ameneŵa amangodzitchera okha msampha, m'menemo muli imfa yao yomwe. Ameneŵa ndiwo mathero a anthu opata chuma mwankhondo. Chumacho chimapha eniake ochikundika. Nzeru ikufuula mu mseu, ikulankhula mokweza mau m'misika. Ikufuula pa mphambano za miseu, ikulankhula pa zipata za mzinda, kuti, “Kodi anthu osachangamukanu, mudzakondwerabe kupusaku mpaka liti? Kodi anthu onyodola, adzakhalabe akunyodola mpaka liti? Nanga opusa adzakana kuphunzira zanzeru mpaka liti? Musamale kudzudzula kwangaku, ine ndikuuzani maganizo anga, ndi kukudziŵitsani mau anga. Paja ine ndidaakuitanani, inu nkukana kumvera, ndidaati ndikuthandizeni, koma popanda wosamalako. Uphungu wanga simudaulabadire, kudzudzula kwanga simudakusamale. Ndiye inenso ndidzakusekani, mukadzagwa m'mavuto, ndidzakunyodolani, mukadzazunguzika ndi mantha, pamene mantha adzakukunthani ngati namondwe, pamene tsoka lidzakufikirani ngati kamvulumvulu, pamene mavuto ndi masautso adzakugwerani. Tsono mudzandiitana, koma ine sindidzaitaŵa, mudzandifunafuna mwakhama, koma simudzandipeza. Popeza kuti mudadana ndi nzeru, ndipo simudasankhe kuwopa Chauta, popeza kuti simudasamale malangizo anga, ndipo mudanyoza kudzudzula kwanga konse, basitu tsono mudzadya zipatso zoyenera ntchito zanuzo, mudzakhuta zoipa zimene munkafuna kuŵachita ena. Anthu opusa amaphedwa chifukwa cha kusokera kwao. Zitsiru zimadziwononga zokha nkudzitama kwao. Koma amene amamvera ine adzakhala pabwino, adzakhala mosatekeseka, osaopa choipa chilichonse”. Mwana wanga, uvomere mau anga, ndi kusunga bwino malamulo anga. Uzitchera khutu ku nzeru, uziikapo mtima pa kumvetsa zinthu. Ndikutitu upemphe mtima wozindikira zinthu, ndi kupemba kuti ukhale womvetsa zinthu. Uziifunafuna nzeruyo ngati siliva, ndi kumaiwunguza ngati chuma chobisika. Ukatero, udzamvetsa za kuwopa Chauta, udzapeza nzeru za kudziŵa Mulungu. Paja Chauta ndiye amapatsa nzeru, Iye ndiye kasupe wa kudziŵa zinthu ndi wa kumvetsa. Amasungira anthu olungama nzeru zenizeni, ali ngati chishango choteteza oyenda mwaungwiro. Ndiye mlonda wa njira zolungama, amatchinjiriza njira ya anthu ake oyera mtima. Motero udzamvetsa za ungwiro ndi chilungamo, za kusakondera, ndi za njira iliyonse yabwino. Nzeru zidzaloŵa mumtima mwako, kudziŵa zinthu kudzakusangalatsa. Kuganiziratu zam'tsogolo kudzakusunga, kumvetsa zinthu kudzakuteteza. Nzeruyo idzakupulumutsa ku mayendedwe oipa, idzakuteteza kwa amtherakuŵiri, amene amasiya njira zolungama, namayenda m'njira zamdima. Iwoŵa amakondwa pochita zoipa, amasangalala ndi ntchito zosalungama. Anthu ameneŵa njira zao nzokhotakhota, makhalidwe ao ngonyenga. Udzapulumuka kwa mkazi wadama, kwa mkazi wachiwerewere wolankhula mau oshashalika, amene amasiya mwamuna wake wapaumbeta, kuiŵala chipangano chochita ndi Mulungu wake. Pakuti nyumba yake imatsenderekera ku imfa, njira zake zimamufikitsa kwa anthu akufa. Opita kwa iye, palibe ndi mmodzi yemwe wobwerako, sazipezanso njira zopita ku moyo. Ndiye iwe, uzitsata njira za anthu abwino, uziyenda m'njira za anthu ochita chilungamo. Paja anthu olungama ndiwo adzakhale m'dziko, anthu okhulupirika ndiwo adzakhazikike m'menemo. Koma anthu oipa Mulungu adzaŵachotsa pa dziko, anthu onyenga adzaŵatulutsa m'dzikomo. Mwana wanga, usaiŵale malangizo angaŵa, koma mtima wako usunge malamulo anga. Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka, ndipo udzakhala ndi moyo wabwino kwambiri. Khalidwe la kudzipereka ndi kukhulupirika zisakuthaŵe, makhalidwe ameneŵa uziyenda nawo ngati mkanda wam'khosi, uŵalembe mumtima mwako. Choncho udzapeza kuyanja ndi mbiri yabwino pamaso pa Mulungu ndi pa anthunso. Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa. Usamadziwona ngati wanzeru. Uziwopa Chauta, ndipo uleke zoipa. Kuchita choncho kudzapatsa thupi lako moyo, kudzalimbitsa mafupa ako. Uzilemekeza nacho Chauta chuma chako chonse, uzimuyamika nazo zokolola zako zonse zam'minda. Ukatero, nkhokwe zako zidzadzaza ndi dzinthu dzambiri, mbiya zako zidzachita kusefukira ndi vinyo. Mwana wanga, usanyoze malango a Chauta, usatope nako kudzudzula kwake. Paja Chauta amadzudzula yemwe amamkonda, monga momwe atate amamchitira mwana wokondwera naye. Ngwodala munthu amene wapeza nzeru, amene walandira nzeru zomvetsa zinthu, pakuti phindu la nzeru nloposa phindu la siliva, nloposanso ndi phindu la golide lomwe. Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali. Palibe chinthu chochilakalaka cholingana ndi nzeruyo. Ndi nzeru imene imakupatsa moyo wautali. Ndi nzeru imene imakuninkha chuma ndi ulemu. Nzeru imakudzeretsa m'njira za chisangalalo, nimakuyendetsa mumtendere mokhamokha. Nzeru ili ngati mtengo woŵapatsa moyo oigwiritsa. Ngodala amene amaikangamira molimbika. Pamene adakhazikitsa dziko lapansi, Chauta adaonetsa nzeru. Pamene adakhazikitsa zakumwamba, adaonetsa nzeru za kumvetsa bwino. Pamene adatumphutsa madzi kuchoka kunsi kwa dziko, ndipo mitambo idagwetsa mvula, adaonetsa nzeru zodziŵa zinthu. Mwana wanga, usunge nzeru yeniyeni usunge mkhalidwe wa kulingalira bwino, ziŵiri zimenezi zisakuthaŵe. Zimenezi zidzakupatsa moyo, moyo wake wokongola ngati mkanda wam'khosi. Tsono udzayenda pa njira yako mosaopa, phazi lako silidzaphunthwa konse. Ukamakhala pansi, sudzachita mantha, ukamagona, udzakhala ndi tulo tabwino. Usamaopa zoopsa zobwera modzidzimutsa, usamachita mantha ndi tsoka lodzagwera anthu oipa. Chauta ndiye adzakhale chikhulupiriro chako, adzasunga phazi lako kuti lingakodwe. Usaleke kumchitira zabwino woyenera kuzilandira, pamene uli nazo mphamvu zochitira choncho. Usamuuze mnzakoyo kuti, “Pita, ukachite kubweranso, ndidzakupatsa maŵa,” pamene uli nazo tsopano lino. Usamkonzekere chiwembu mnzako, amene amakhala nawe pafupi mokudalira. Usamakangane ndi munthu popanda chifukwa pamene iyeyo sadakuchite choipa chilichonse. Usachite naye nsanje munthu wachiwawa, usatsanzireko khalidwe lake lililonse. Paja Chauta amanyansidwa ndi munthu woipa, koma olungama okha amayanjana nawo. Chauta amatemberera nyumba ya anthu oipa, koma malo okhalamo anthu abwino amaŵadalitsa. Anthu onyoza, Iye amaŵanyoza, koma odzichepetsa Iye amaŵakomera mtima. Anthu anzeru adzalandira ulemu, koma zitsiru adzazichititsa manyazi. Ana inu, mverani malangizo a atate anu, tcherani khutu, kuti mupate nzeru zodziŵira zinthu. Ine ndikukupatsani malamulo abwino, musasiye zimene ndikukuphunzitsani. Pamene ndinali mwana m'nyumba mwa atate anga, m'menemo ndili kamwana kapamtima ka amai anga, atatewo adandiphunzitsa ndi mau akuti, “Ugwiritse mumtima mwako zimene ndikukuuzazi, usunge malamulo anga, kuti ukhale ndi moyo. Usaiŵale mau a pakamwa pangaŵa, usatayane nawo, Ukhale ndi nzeru, ndiponso khalidwe la kumvetsa zinthu. Usaisiye nzeru, ndipo idzakusunga. Uziikonda, ndipo idzakuteteza. Chachikulu pa nzeru ndi ichi: Kaya nchiyani chimene ungapate, peza nzeruyo, usalephere kupata khalidwe la kumvetsa zinthu. Uziilemekeza nzeruyo, ndipo idzakukweza. Uifungate ndipo idzakupatsa ulemerero. Idzaika pamutu pako nsangamutu yokongola yamaluŵa. Idzakuveka chisoti chaufumu chaulemu.” Mwana wanga, umvere ndi kuvomera zimene ndikunena. Ukatero, zaka za moyo wako zidzachuluka. Ndakuphunzitsa njira yake ya nzeru. Ndakutsogolera pa njira za moyo wolungama. Ukamayenda, mapazi ako sazidzaombana. Ukamathamanga, sudzakhumudwa ai. Uŵasamale zedi, pakuti moyo wako wagona pamenepo. Usayende m'njira za anthu oipa, usatsate m'mapazi mwa anthu ochimwa. Njira zao uzipewe, usapitemo konse. Uzilambalale, ndi kungozipitirira. Iwo ajatu sangagone, mpaka atachita ndithu choipa. Tulo sangatiwone, mpaka atakhumudwitsapo munthu. Paja kuchita zoipa ndiye chakudya chao, kuchita ndeu ndiye chakumwa chao. Koma njira ya anthu okondweretsa Mulungu, ili ngati kuŵala kwa mbandakucha, kumene kumanka kukukulirakulira mpaka dzuŵa litafika pamutu. Njira ya anthu oipa ili ngati mdima wandiweyani. Satha kuzindikira kuti aphunthwa pa chiyani. Mwana wanga, mvetsetsa mau anga. Tchera khutu ku zimene ndikunena. Zisachoke m'mutu mwakomu, uzisunge bwino mumtima mwako. Paja zimampatsa moyo amene wazipeza, zimachiritsa thupi lake lonse. Mtima wako uziwulonda bwino, pakuti m'menemo ndimo muli magwero a moyo. Ulekeretu kulankhula zokhotakhota, usiyiretu kukamba zopotoka. Maso ako aziyang'ana kutsogolo molunjika, uzipenya kutsogolo osacheukacheuka. Uzisamala m'mene mukupita mapazi ako, ndipo njira zako zonse zidzakhala zosapeneketsa. Usapatukire kumanja kapena kumanzere, usayende pamene pali choipa chilichonse. Mwana wanga, umvetsere bwino zanzeru ndikukuuzazi, utchere khutu kwa ine womvetsa bwino zinthu, kuti uziganiza mochenjera, ndipo pakamwa pako pazilankhula zanzeru. Paja mkazi wadama ali ndi pakamwa pokoma ngati uchi, mau ake ndi osalala koposa mafuta. Koma kotsiriza kwake ngwoŵaŵa ngati chivumulo, ngwolasa ngati lupanga lakuthwa konsekonse. Mapazi ake ndi oloza ku imfa, poyenda amaloŵera njira yakumanda. Njira yamoyo saisamala mpang'ono pomwe. Njira zake nzokhotakhota, koma mwiniwakeyo sadziŵako. Tsopano, ana inu, mundimvere ine, musaŵataye mau a pakamwa panga. Uzilambalala kutali ndi mkazi wotere, usamafika kufupi ndi khomo la nyumba yake. Mwinamwina ulemu wako udzalanditsa kwa ena, zaka zako zaunyamata udzazitaya kwa anthu ankhanza. Mwinanso alendo adzadyerera chuma chako, phindu la ntchito zako lidzagwa m'manja mwa munthu wachilendo. Ndipo potsiriza pa moyo wako udzalira chokuwa, thupi lako lonse litatheratu. Pamenepo iwe udzangoti, “Kalanga ine, ndinkadana nkusunga mwambo, mtima wanga unkanyoza chidzudzulo! Sindidamvere mau a aphunzitsi anga, sindidatchere khutu kwa alangizi anga. Pang'onong'ono, bwenzi nditaonongekeratu pakati pa mpingo wonse utasonkhana.” Iwe, uzimwera m'chitsime chakochako, ndiye kuti khala wokhulupirika kwa mkazi wako. Kodi ana ako azingoti mbwee ponseponse ngati madzi ongoyenda m'miseu? Anawo akhale a iwe wekha, osatinso uŵagaŵane ndi alendo. Uzikhutira ndi mkazi wako, uzikondwa ndi mkazi wa unyamata wako. Iye uja ngwokongola ngati mbaŵala, ndi wa maonekedwe osiririka ngati mbalale. Uzikhutitsidwa ndi maŵere ake nthaŵi zonse, uzikokeka ndi chikondi chake pa moyo wako wonse. Mwana wanga, ungakopekerenji ndi mkazi wadama, ungamkumbatire bwanji mkazi wosakhala wako? Mayendedwe a munthu Chauta amaŵaona bwino lomwe, njira zake zonse amazipenyetsetsa. Zoipa za munthu woipa zimamtchera msampha iyeyo, ntchito za machimo ake zimamkwidzinga. Amafa chifukwa chosoŵa mwambo, amatayika chifukwa cha uchitsiru wake waukulu. Mwana wanga, kodi udalonjeza kumlipirira mnzako chikole, kodi udaperekera mlendo chigwiriro? Kodi udakodwa ndi mau a pakamwa pako pomwe, kodi udagwidwa ndi mau olankhula iwe wemwe? Ndiye iwe mwana wanga, popeza kuti wadziponya m'manja mwa mnzako, chita izi kuti udzipulumutse: nyamuka, pita msanga, ukampemphe kuti akumasule. Usagone tulo, usaodzere, Dzipulumutse monga imadzipulumutsira mphoyo kwa mlenje, monga imadzipulumutsira kwa wosaka. Pita kwa nyerere, mlesi iwe. Kapenyetsetse makhalidwe ake, ukaphunzireko nzeru. Ilibe ndi mfumu yomwe, ilibe kapitao kapena wolamulira. Komabe imakonzeratu chakudya chake m'malimwe, ndipo imatuta chakudyacho m'masika. Kodi ukhalabe uli gone pamenepo mpaka liti, mlesi iwe? Kodi titha liti tulo takoto? Ukati ndingogonako pang'ono, ndingoodzerako pang'ono chabe, ndingopinda manja okhaŵa kuti ndipumuleko, umphaŵi udzakugwira ngati munthu wachifwamba, usiŵa udzakufikira mwadzidzidzi ngati mbala. Munthu wachabechabe, munthu woipa, amangoyendayenda nkumalankhula zabodza. Amatsinzinira masoŵa nkumakwekwesa pansi mapazi ake, amalozaloza ndi chala chake. Amalingalira zoipa ndi mtima wake wopotoka, amangokhalira kuvundula madzi pakati pa anthu. Nchifukwa chake tsoka lidzamgwera modzidzimutsa. Pa kamphindi kochepa adzaonongedwa, osapulumuka konse. Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Chauta amadana nazo, makamaka zisanu ndi ziŵiri ndithu zimene zimamunyansa: maso onyada, pakamwa pabodza, manja opha munthu wosalakwa, mtima wokonzekera kuchita zoipa, mapazi othamangira msangamsanga ku zoipa, mboni yonama yolankhula mabodza, ndi munthu woutsa chidani pakati pa abale. Mwana wanga, uzitsata malamulo a atate ako, usasiye zimene adakuphunzitsa amai ako. Zimenezi uzimatirire pamtima pako masiku onse, uzimangirire m'khosi mwako. Pamene ukuyenda, zidzakulozera njira. Pamene ukukhala chogona, zidzakulonda. Pamene ukudzuka, zidzakulangiza. Paja malamulowo ali ngati nyale, maphunzitsowo ali ngati kuŵala, madzudzulo a mwambo aja ndiwo mkhalidwe weniweni pa moyo wa munthu. Zimenezi zidzakupulumutsa kwa mkazi woipa, zidzakuthandiza kuti usamvere mau osalala a mkazi wachiwerewere. Mumtima mwako usamakhumbira kukongola kwake, usakopeke nawo maso ake. Paja mkazi wachiwerewere ungathe kumgula ndi buledi, koma wadama wokwatiwa amakulanda ndi moyo wako womwe. Kodi munthu angathe kufukata moto, zovala zake osapsa? Kodi munthu angathe kuponda makala amoto, mapazi ake osapserera? Ndizo zimamchitikira wokaloŵerera mkazi wamwini. Aliyense wokhudza mkazi wotero adzalangidwa. Paja anthu sainyoza mbala, ikaba chifukwa cha njala. Komabe ikangogwidwa, imalipira kasanunkaŵiri, mpaka mwina kulandidwa katundu yense wa m'nyumba mwake. Amene amachita chigololo ndi wopanda nzeru, amangodziwononga yekha. Adzangolandira mabala ndi manyozo, ndipo manyazi ake sadzamchoka ai. Paja nsanje imakalipitsa mwini mkaziyo, sachita chifundo akati alipsire. Savomera dipo lililonse, sapepeseka ngakhale umpatse mphatso zochuluka chotani. Mwana wanga, mvera mau anga, malamulo anga akhale chuma chako. Utsate malamulo anga, ndipo udzakhala ndi moyo. Usamale malangizo anga monga umachitira ndi maso ako. Achite ngati waŵamangirira ku chala, ngati waŵadinda mumtima mwako. Nzeru uiwuze kuti, “Iwe ndiwe mlongo wanga,” ndipo khalidwe la kumvetsa zinthu ulitchule kuti, “Bwenzi langa lapamtima.” Zikuteteze kwa mkazi wadama, ku mau oshashalika a mkazi wosakhala wako. Tsiku lina pa windo la nyumba yanga, ndidasuzumira pa made, ndipo pakati pa anthu opusa, pakati pa achinyamata, ndidaona wachinyamata mmodzi wopanda nzeru. Ankayenda m'njira pafupi ndi nyumba ya mkaziyo, ankaphera mu mseu wa kunyumba kumeneko. Inali nthaŵi ya chisisira, madzulo, nthaŵi yausiku, kuli mdima. Ndiye mkazi adadzakumana naye, atavala ngati mkazi wadama, wa mtima wonyenga. Mkaziyo ndi wosakhazikika ndi wopanda manyazi, kamwendom'njira wosakhala pakhomo. Mwina umpeza pa mseu, mwina pa msika, amachita kukhalizira munthu pa mphambano iliyonse. Tsono amamgwira mnyamata uja, nkumumpsompsona, amalankhula naye ndi nkhope yopanda manyazi kunena kuti, “Ndinayenera kupereka nsembe, ndipo lero ndachita zimene ndidazilumbirira. Motero tsopano ndabwera kuti ndidzakumane nawe, ndinkakufunafuna, tsono ndakupeza. Pabedi panga ndayalapo zofunda zabwino, pali nsalu zabafuta zamaŵangamaŵanga za ku Ejipito. Pomweponso ndawazapo zonunkhira za mure, ndi mankhwala a fungo lokoma a aloyi, ndi a sinamoni. Bwera tsono, tikhale malo amodzi mpaka m'maŵa, tisangalatsane ndi chikondi. Mwamuna wanga kulibe, ali pa ulendo wautali. Adatenga thumba la ndalama, adzabwerako mwezi utakhwima.” Amamkopa mnyamatayo ndi mau onyengerera, amamkakamiza ndi mau ake oshashalika. Pamenepo mnyamatayo amatsatira mkaziyo monga momwe ng'ombe imapitira kokaphedwa, kapena monga momwe mbaŵala imakodwera mu msampha, mpaka muvi kuilasa m'mimba mwake. Amakhala ngati mbalame yothamangira m'khwekhwe, osadziŵako kuti aferapo. Ndiye tsopano ana inu, mundimvere ine, mutchere khutu pa zimene ndinene ine. Musatengeke mtima ndi njira za mkazi ameneyo, musasokere potsata njira zakezo. Paja iye uja adagwetsa amuna ambiri, anthu amene adaŵaphetsa ngosaŵerengeka. Nyumba yake ndi njira yakumanda, yotsikira ku dziko la anthu akufa. Kodi suja nzeru imaitana? Suja nzeru zomvetsera zinthu zimakweza mau ake? Nzeru imakhala pa zitunda m'mbali mwa njira, imakaima pa mphambano za miseu. Imafuula pafupi ndi zipata kumaso kwa mzinda, ndiponso pamakomo poloŵera, imati, “Inu anthu, ndikukuitanani, kuitanaku ndikuitana anthu nonsenu. Inu osadziŵa kanthunu, phunzirani nzeru, inu opusanu, khalani tcheru. Mverani, ndikuuzani zazikulu kwambiri, pakamwa panga palankhula zolungama. Pakamwa panga palankhula zoona, kulankhula zoipa nchinthu chonyansa m'kamwa mwanga. Mau onse a pakamwa panga ngokondweretsa Mulungu, m'mau angawo mulibe zopotoka kapena zokhotakhota. Mau anga ngoona kwa munthu womvetsa, ngokhoza kwa anthu odziŵa zinthu. Landirani malangizo anga m'malo mwa siliva, funitsitsani kudziŵa zinthu, osati kuthamangira golide wabwino kwambiri. Nzerutu ndi yabwino kuposa miyala yamtengowapatali. Zonse zimene ungazilakelake sizingafanefane ndi nzeru. Ine nzeru ndimakhalira limodzi ndi kuchenjera. Ndimadziŵa zinthu ndipo ndimaganiza moyenera. Kuwopa Chauta nkudana ndi zoipa. Kunyada, kudzitama, kuchita zoipa ndi kulankhula zonyenga, zonsezo ndimadana nazo. Ndili ndi uphungu ndi maganizo abwino. Ndimamvetsa bwino zinthu, ndilinso ndi mphamvu. Ndimathandiza mafumu polamulira ndine, olamulira ndimaŵathandiza ndine kulamula zolungama. Ndine ndimathandiza akalonga polamula, ndine ndimathandiza akuluakulu poweruza m'dziko. Anthu ondikonda, ine nzeru ndimaŵakonda, anthu ondifunafuna mosamala, amandipeza. Ndili nacho chuma, ndili nawo ulemu, chuma chosatha ndiponso kukhuphuka konkirankira. Zimene mumalandira kwa ine nzokoma kuposa golide, ngakhale golide wosalala. Phindu lochokera mwa ine nloposa siliva wabwino zedi. Ndimachita zomwe zili zoyenera, sindipatuka kuchoka m'njira za chilungamo. Ndimaŵapatsa chuma anthu ondikonda, ndi kudzaza nyumba zao zosungiramo chuma. “Chauta adandilenga ine nzeru pa chiyambi cha ntchito zake. Mwa ntchito zake zakalekale woyambirira ndinali ine. Ndidapangidwa masiku akalekale, pachiyambiyambi, dziko lapansi lisanalengedwe. Nyanja zozama zisanalengedwe, padakalibe akasupe odzaza ndi madzi, nkuti ine nditabadwa kale. Mapiri asanaumbidwe, magomo asanakhalepo, Mulungu anali atandilenga ineyo; lisanalengedwe dziko lapansi ndi minda yake, lisanakhaleponso dothi loyamba la dziko lapansi. Ine ndinalipo kale, pamene ankakhazikitsa zakumwamba, pamene ankalemba mzere wa malire a nyanja yozama, pamene ankaika thambo m'malo mwake, pamene ankatsekula akasupe a m'nyanja yozama, pamene ankaika malire a nyanja kuti madzi ake asabzole malirewo, pamene ankaika maziko a dziko lapansi. Nthaŵiyo nkuti ndili pambalipa ngati mmisiri wake, ndikumkondweretsa tsiku ndi tsiku, ndikusangalala pamaso pake nthaŵi zonse. Ndinkasangalala m'dziko lake lokhalamo anthu, ndi kumakondwa nawo ana a anthu. “Ndipo tsopano, ana anga, tamverani, ngodala anthu amene amasunga malangizo anga. Muzimva malangizo, kuti muzikhala anzeru, musamanyozere mau anga. Ngwodala munthu amene amatchera khutu kwa ine, amene amakhala pakhomo panga tsiku ndi tsiku, amene amadikira pa chitseko changa. Paja wondipeza ine, wapeza moyo, ndipo amapeza kuyanja pamaso pa Chauta. Koma wosandipeza ine, akudzipweteka ameneyo. Onse odana ndi ine, ngokonda imfa amenewo.” Nzeru idamanga nyumba yake, idaimika nsanamira zake zisanu ndi ziŵiri. Idapha ziŵeto zake, idakonza vinyo wake, nkuyala tebulo lake. Idatuma adzakazi ake kuti akakhalire pa malo apamwamba mu mzinda ndipo akalengeze kuti, “Munthu wamba aliyense abwere kuno!” Kwa munthu wopanda nzeru imati, “Bwera, dzadyeko chakudya changa, ndipo udzamweko vinyo amene ndakonza. Leka kupulukira kwako, kuti ukhale ndi moyo, uziyenda m'njira ya nzeru.” Woyesa kukonza munthu wonyoza, amangonyozekerapo, wodzudzula munthu woipa, amangopwetekerapo. Wonyoza usamdzudzule, angadane nawe. Koma ukadzudzula munthu wanzeru, adzakukonda. Wanzeru ukamlangiza, adzakhala wanzeru koposa. Munthu wochita chilungamo ukamuphunzitsa, adzadziŵa zambiri koposa. Kulemekeza Chauta ndiye chiyambi cha nzeru, kudziŵa Woyera uja nkukhala womvetsa bwino zinthu. Chifukwa cha ine nzeru, masiku ako adzachuluka, ndipo ndidzaonjezera zaka pa moyo wako. Ngati ndiwe wanzeru, phindu ndi lako. Ngati umanyoza ena, udzavutika ndiwe wekha. Mkazi wopusa ngwaphokoso, ngwosachangamuka, ndiponso wosamvetsa zinthu. Amakhala pakhomo pa nyumba yake, pamalo pena pooneka bwino mu mzinda. Akatero nkumaitana amene akudutsapo, amene akungodziyendera, osafuna kupatuka. “Amati, inu anthu wamba, tapatukirani muno!” Tsono kwa wopanda nzeru amati, “Madzi akuba ndiwo amatsekemera, buledi wodya mobisa ndiye amakoma.” Koma mwamunayo sadziŵa kuti kumeneko kuli imfa, kuti alendo ake aloŵa kale m'manda ozama. Miyambo ya Solomoni: Mwana wanzeru amakondweretsa atate ake, koma mwana wopusa amanyoza amai ake. Chuma chochipeza monyenga sichipindulitsa, koma chilungamo chimapulumutsa ku imfa. Chauta salola kuti munthu womukondweretsa iye, azikhala ndi njala, koma zimene woipa amazilakalaka, Mulungu amam'mana. Manja aulesi amagwetsa munthu mu umphaŵi, koma manja achangu amalemeretsa munthu. Mwana womakolola nthaŵi yachilimwe ndiye wanzeru, koma womangogona nthaŵi yokolola amachititsa manyazi. Madalitso amakhala pa munthu wokondweretsa Mulungu, koma pakamwa pa munthu woipa pamabisa zandeu. Munthu wabwino anzake adzamkumbukira ngati dalitso, pamene woipa, mbiri yake idzatha ngati chinthu choola. Munthu wa mtima wanzeru adzasamala malamulo, koma chitsiru chomangolongolola chidzaonongeka. Munthu woyenda mwaungwiro, amayenda mosatekeseka. Koma woyenda njira zoipa, adzadziŵika. Munthu wotsinzinira maso monyenga, amadzetsa mavuto, wodzudzula molimba mtima amadzetsa mtendere. Pakamwa pa munthu wabwino ndi kasupe wa moyo, koma pakamwa pa munthu woipa pamabisa zandeu. Chidani chimautsa mikangano, koma chikondi chimaphimba zolakwa zonse. Pakamwa pa munthu womvetsa zinthu pamatuluka zanzeru, koma pamsana pa munthu wopanda nzeru sipachoka tsatsa. Anzeru amakundika nzeru, koma kubwebwetuka kwa chitsiru kumadzetsa chiwonongeko. Chuma cha munthu wolemera ndiye chitetezo chake, koma umphaŵi wa anthu osauka ndiye chiwonongeko chao. Moyo ndiye malipiro a anthu ochita zabwino, koma phindu la ochimwa limadzetsa machimo ena. Wosamala malangizo amayenda pa njira ya moyo, koma wokana chidzudzulo amasokera. Wobisa chidani chake ndi munthu wonama, ndipo wochita ugogodi nchitsiru. Mau akachuluka, zolakwa sizisoŵa, koma amene amasunga pakamwa ndi wanzeru. Mau a munthu wochita zabwino, ali ngati siliva wabwino kwambiri, koma maganizo a anthu oipa ngachabe. Mau a anthu wabwino amaphunzitsa ambiri, koma zitsiru zimafa chifukwa chosoŵa nzeru. Madalitso a Chauta ndiwo amalemeretsa, ntchito za munthu siziwonjezerapo kanthu. Kwa chitsiru kulakwa kumakhala ngati maseŵera, koma kwa munthu womvetsa zinthu kuchita zanzeru ndiye kumapatsa chimwemwe. Chimene woipa amachiwopa chidzamgwera, koma zimene munthu wabwino amazilakalaka adzazipeza. Namondwe akaomba, oipa amachotsedwa, koma anthu ochita chilungamo amakhazikika mpaka muyaya. Momwe amakhalira vinyo wosasa m'kamwa, momwe umakhalira utsi m'maso, ndi momwenso amakhalira mlesi kwa amene amamtuma. Kuwopa Chauta kumatalikitsa moyo, koma zaka za anthu oipa zidzachepa. Chiyembekezo cha wokhulupirira chimapezetsa chimwemwe, koma zimene woipa amayembekezera, zimafera m'mazira. Chauta ndi linga loteteza munthu woyenda molungama, koma amaononga wochita zoipa. Munthu wabwino sadzachotsedwa pamalo pake, koma woipa sadzakhazikika pa dziko. Pakamwa pa wochita chilungamo pamatuluka zanzeru, koma lilime lokhota adzalidula. Anthu omvera Mulungu amadziŵa zoyenera kulankhula, koma pakamwa pa anthu oipa pamatuluka zosayenera. Muyeso wonyenga umanyansa Chauta, koma muyeso wachilungamo umamkondweretsa. Kunyada kukaloŵa, pamafikanso manyazi, koma pali kudzichepetsa, palinso nzeru. Ungwiro wa anthu olungama umaŵatsogolera, koma makhalidwe okhota a anthu onyenga ngoononga. Pa tsiku la mkwiyo wa Mulungu chuma sichithandiza konse, koma chilungamo ndiye chimapulumutsa ku imfa. Kulungama kwa anthu angwiro kumaŵathandiza pa moyo wao, koma kuipa mtima kumagwetsa mwiniwake yemweyo. Kulungama kwa munthu woyera mtima kumampulumutsa, koma zilakolako zoipa zimaŵaika mu ukapolo anthu onyenga. Woipa akafa, chikhulupiriro chake chimathanso, chiyembekezo cha wosasamala za Mulungu chilibe phindu. Anthu a Mulungu amapulumuka ku mavuto, koma m'malo mwake amagwamo ndi oipa mtima. Munthu wosalabadirako za Mulungu amaononga mnzake ndi pakamwa pake; munthu wochita chilungamo amapulumuka chifukwa cha kudziŵa zinthu. Mulungu akamadalitsa anthu ake, mzinda wonse umatukuka. Oipa akaonongeka, anthu amafuula mwachimwemwe. Madalitso olandira anthu olungama amakweza mzinda, koma pakamwa pa anthu oipa mtima pamapasula mzindawo. Wosukitsa anzake ngwopanda nzeru, koma womvetsa zinthu amalonda pakamwa pake. Amene amanka nachita ukazitape, amaulula zinsinsi. Koma wa mtima wokhulupirika, amasunga pakamwa pake. Kumene kulibe uphungu, anthu amagwa, koma kumene kuli aphungu ambiri, kumakhala mtendere. Woperekera wachilendo chigwiriro, adzapeza mavuto, koma wodana ndi za chigwiriro, amakhala pa mtendere. Mkazi wa mkhalidwe wabwino amalandira ulemu, koma amuna ankhanza amangopata chuma. Munthu wachifundo amadzipindulira zabwino, koma munthu wankhwidzi amadzipweteka yekha. Munthu woipa amalandira malipiro achabechabe, koma wochita zolungama amalandira mphotho yeniyeni. Wofunitsitsa chilungamo, adzakhala moyo. Koma wothamangira zoipa, adzafa. Anthu a mtima woipa amamnyansa Chauta, koma anthu a makhalidwe abwino amamkondweretsa. Zoonadi, anthu oipa chilango sichidzamuphonya, koma anthu a Mulungu adzapulumuka. Momwe chimaonekera chipini chagolide chikakhala pa mpuno wa nkhumba, ndi momwenso kumakhalira kukongola kwa mkazi wam'kamwa. Zimene anthu abwino amazilakalaka zimathera mwabwino, koma zimene oipa amayembekezera zimathera ku mkwiyo wa Mulungu. Wina amatha kupatsako anzake zinthu mwaufulu, komabe amanka nalemereralemerera. Wina nkukhala wakaligwiritsa, nakhalabe wosauka. Munthu wa mtima waufulu adzalemera, wothandiza anzake nayenso adzalandira thandizo. Anthu amatemberera munthu womana anzake chakudya, koma amalemekeza munthu wogulitsa chakudyacho. Munthu wofunafuna zabwino mwakhama, amapeza zokoma, koma wofunafuna zoipa, zidzampeza. Wokhulupirira chuma chake adzafota, koma anthu a Mulungu adzaphukira ngati tsamba laliŵisi. Wovutitsa a m'nyumba mwake adzaloŵa m'mavuto, chitsiru chidzasanduka kapolo wa munthu wanzeru. Kukhala moyo wangwiro kumapezetsa moyo, koma kusatsata malamulo kumaononga moyo. Anthu abwino amalandira mphotho pa dziko lapansi, koma wochimwa ndi woipa mtima amalandira chilango. Munthu wokonda mwambo amakonda kudziŵa zinthu, koma wodana ndi chidzudzulo ngwopusa. Munthu wabwino amapeza kuyanja pamaso pa Chauta, koma munthu wokonzekera zoipa, Chauta amamzenga mlandu. Munthu sakhazikika bwino pochita uchimo, koma maziko a munthu wochita zabwino sadzagwedezeka. Mkazi wabwino ali ngati chisoti chaulemu kwa mwamuna wake, koma mkazi wochititsa manyazi ali ngati chilonda chamafinya kwa mwamuna wake. Maganizo a munthu wabwino ngoongoka, koma malangizo a munthu woipa ngonyenga. Mau a munthu woipa mtima ngophetsa, koma mau a munthu wolungama ngopulumutsa anthu. Anthu oipa mtima amagwetsedwa, naiŵalika, koma banja la anthu omvera Mulungu silidzapasuka. Munthu amamuyamika malinga ndi nzeru zake, koma munthu wa mtima wokhota amanyozeka. Munthu wamba, wodzigwirira ntchito napeza zofunika, ali pabwino kuposa wongodzikuza, pamene alibe nchakudya chomwe. Munthu wolungama amasamalira moyo wa ziŵeto zake, koma munthu woipa mtima chifundo chake nchankhwidzi. Wolima munda wake mwakhama amapeza chakudya chambiri, koma wotsata zopanda pake ngwopanda nzeru. Nsanja yolimba ya anthu oipa mtima imaonongeka, koma maziko a munthu wabwino ngosagwedezeka. Munthu woipa amakodwa mu msampha wa zoipa za pakamwa pake, koma munthu wochita zabwino amapulumuka ku zoipa. Munthu amalandira zabwino zambiri chifukwa cha mau ake abwino, ntchito zimene munthu amazichita ndi manja ake zimampindulira. Zimene amachita munthu wopusa mwiniwakeyo amaziyesa zolungama, koma munthu wanzeru amamvetsera malangizo a ena. Kukwiya kwa munthu wopusa kumadziŵika msanga, koma munthu wanzeru salabadako za chipongwe. Wolankhula zoona amapereka umboni woona, koma mboni yonama imalankhula monyenga. Wofulumira kulankhula, zonena zake zimalasa ngati mpeni, koma mau a munthu wanzeru amachiza anzake. Mau oona amakhala mpaka muyaya, koma zabodza sizikhalitsa. Mumtima mwa anthu opangana zoipa mumakhala kunama, koma anthu olinga zabwino amakhala ndi chimwemwe. Munthu wabwino vuto silimgwera, koma woipa mavuto samchoka. Pakamwa pabodza pamamnyansa Chauta. Koma anthu ochita zinthu mokhulupirika amamkondweretsa. Munthu wochenjera amabisa nzeru zake, koma anthu opusa amaonetsa poyera kupusa kwao. Ogwira ntchito mwakhama adzakhala olamulira, koma aulesi adzakhala akapolo. Nkhaŵa ya munthu imakhala ngati katundu wolemera mumtima mwake, koma mau abwino amamsangalatsa. Munthu wochita zabwino amatsogolera anzake pa njira yokhoza, koma njira ya munthu woipa imaŵasokeretsa. Munthu waulesi sapeza zimene akukhumba, koma munthu wakhama amapeza chuma chamtengowapatali. Njira ya chilungamo imafikitsa ku moyo, koma njira ya zoipa imafikitsa ku imfa. Mwana wanzeru amamvera malangizo a atate ake, koma wonyoza samvetsera akamamdzudzula. Munthu wabwino amapeza nako phindu kulankhula kwake, koma anthu onyenga amalakalaka zandeu. Amene amagwira pakamwa pake amasunga moyo wake, koma amene amangolakatika amaonongeka. Munthu waulesi amakhumbira zinthu koma sapeza kanthu, m'menemo munthu wakhama amalemera. Munthu wokonda Mulungu amadana ndi bodza, koma zochita za munthu woipa zimanyansa ndipo zimachititsa manyazi. Chilungamo chimatchinjiriza munthu wabwino, koma tchimo limagwetsa munthu woipa. Wina amadziyesa wolemera, m'menemo alibe nkanthu komwe. Wina amadziyesa wosauka, m'menemo ali nchuma chochuluka. Chuma cha munthu wolemera nchimene chimaombola moyo wake, koma munthu wosauka alibe choti nkumuwombola. Kuŵala kwa anthu a Mulungu kumachita kuti ngwee, koma nyale ya anthu oipa mtima siidzalephera kuzima. Chipongwe cha osasamala za anzao chimadzetsa mkangano, koma omvera malangizo a anzao ndiwo ali ndi nzeru. Chuma chochipeza mofulumira chidzanka chitha pang'onopang'ono, koma chochipeza pang'onopang'ono chidzanka chichulukirachulukira. Chinthu chochiyembekeza chikalephereka, chimafooketsa mtima, koma chinthu chochilakalaka chikachitikadi, chili ngati mtengo wopatsa moyo. Wonyoza malangizo amadziwononga, koma wosamala lamulo amalandira mphotho. Maphunzitso a anthu anzeru ali ngati kasupe wa moyo, amathandiza anthu kuti asakodwe mu msampha wa imfa. Munthu wa nzeru zabwino, anthu amamkomera mtima, koma munthu wosakhulupirika, kwake nkuwonongeka. Munthu wochenjera amachita zonse mwanzeru, koma wopusa amaonetsa poyera uchitsiru wake. Wamthenga woipa amagwetsa anthu m'mavuto, koma mtumwi wokhulupirika amadzetsa mtendere. Umphaŵi ndi manyazi zimagwera wonyozera mwambo, koma munthu womvera chidzudzulo amalemekezeka. Chinthu chochilakalaka chikachitikadi, chimasangalatsa mtima. Koma kuleka zoipa kuli ngati chinthu chonyansa kwa zitsiru. Woyenda ndi anthu anzeru nayenso amakhala ndi nzeru, koma woyenda ndi zitsiru adzaonongeka. Choipa chitsata mwini, koma wochita chilungamo amalandira zabwino. Munthu wabwino amasiyira zidzukulu zake choloŵa, koma chuma cha munthu woipa amachilandira ndi anthu abwino. M'tsala la munthu wosauka mumalola chakudya chambiri, koma anthu opanda chilungamo amalanda chakudyacho. Amene sakwapula mwana wake, ndiye kuti samkonda, koma amene amakonda mwana wake, sazengereza kumlanga. Munthu wabwino ali nazo zokwanira zoti adye nkukhuta, koma m'mimba mwa munthu woipa mumakhala pululu ndi njala. Mkazi wanzeru amamanga banja lake, koma wopusa amalipasula ndi zochita zake zomwe. Woyenda molungama amaopa Chauta, koma woyenda mokhotakhota amanyoza Chauta. Kulankhula kwa chitsiru kumamuitanira ndodo pa msana, koma mau a munthu wanzeru amamteteza. Kopanda ng'ombe, kumakhalanso kopanda dzinthu, koma kwa ng'ombe zamphamvu, dzinthu dzimachuluka. Mboni yokhulupirika siinama, koma mboni yonyenga imalankhula zabodza. Wonyoza anzake amafunafuna nzeru osaipeza, koma munthu womvetsa amadziŵa bwino zinthu msanga. Usayandikirepo pamene pali chitsiru, paja pamenepo supezapo mau anzeru. Nzeru za munthu wochenjera zagona pa kuzindikira bwino njira zake, koma zitsiru zimanyengedwa nkupusa kwao komwe. Zitsiru sizilabadako za kulapa machimo ao, kufuna kwabwino kumapezeka mwa anthu olungama. Mtima umadziŵa wokha zoŵaŵa zake, ndipo palibe wina angadziŵe kukondwa kwake. Nyumba ya munthu woipa idzapasuka, koma hema la munthu wolungama lidzakhazikika. Pali njira ina yooneka ngati yabwino kwa munthu, koma kopherezera kwake nku imfa. Ngakhale poseka, mtima nkumvabe chisoni, ndipo mathero a chimwemwe ndi chisoni. Munthu wosalungama adzalandira zoyenerera ntchito zake, koma munthu wabwino adzalandira mphotho ya ntchito zake. Munthu wopusa amakhulupirira chilichonse, koma wochenjera amayang'ana m'mene akuyendera. Munthu wanzeru ngwochenjera, ndipo amalewa choipa, koma chitsiru chimadudukira zinthu mosasamalako. Munthu wopsa mtima msanga amachita zauchitsiru, wa khalidwe lonyenga, anthu amadana naye. Anthu opusa wao ndi uchitsiru, koma ochenjera yao ndi mphotho ya kudziŵa zinthu. Anthu ochimwa adzaŵeramira anthu abwino, anthu oipawo adzapempha thandizo kwa abwinowo. Mmphaŵi ngakhale anzake omwe samukonda, koma wolemera amakhala ndi abwenzi ambiri. Amene amanyoza mnzake ngwochimwa, koma ngwodala amene amachitira chifundo amphaŵi. Kodi amene amakonzekera zoipa sachimwa? Koma amene amakonzekera zabwino anthu amaŵaonetsa chifundo ndi kukhulupirika. Pa ntchito iliyonse pali phindu lake, koma kumangolakatika kumabweretsa umphaŵi. Mphotho ya anthu anzeru ndi nzeru zao zomwe, koma anthu opusa malipiro ao ndi uchitsiru wao. Mboni yokhulupirika imapulumutsa anthu, koma mboni yonama imaphetsa. Munthu woopa Chauta ali ndi chikhulupiriro cholimba, ndipo ana ake adzakhala napo pothaŵira. Kuwopa Chauta ndiye kasupe wa moyo, kumapewetsa misampha ya imfa. Chinamtindi cha anthu ndiye ulemerero wake wa mfumu, koma anthu akasoŵa, ufumu wake umasanduka wachabechabe. Wosapsa mtima msanga amamvetsa zinthu kwambiri, koma wofulumira kupsa mtima amaonetsa uchitsiru wake. Mtima wodekha umapatsa thupi moyo, koma nsanje imaoletsa mafupa. Wopondereza mmphaŵi, amachita chipongwe Mlengi wake, koma wochitira chifundo osauka, amalemekeza Mlengi wake. Anthu ochita zoipa amatayika, koma ochita zabwino amatetezedwa. Nzeru zimakhala mumtima mwa anthu omvetsa zinthu, koma mumtima mwa zitsiru sizipezeka. Chilungamo chimakweza mtundu wa anthu, koma uchimo umachititsa manyazi mtundu uliwonse. Mfumu imakondwa ndi mtumiki wochita zinthu mwanzeru, koma imakwiyira wochita zinthu mochititsa manyazi. Kuyankha kofatsa kumazimitsa mkwiyo, koma mau ozaza amakolezera ukali. Mau a anthu anzeru amapatsa nzeru, koma pakamwa pa opusa pamatulutsa zauchitsiru. Maso a Chauta ali ponseponse, amayang'ana oipa ndi abwino omwe. Mau ofatsa amakhala ngati mtengo wopatsa moyo, koma mau oipa amapweteka mtima. Chitsiru chimanyoza malangizo a bambo wake, koma wochenjera amamvera chidzudzulo. Munthu wochita chilungamo amakhala ndi chuma chambiri, koma zimene woipa amapindula zimamgwetsa m'mavuto. Pakamwa pa anthu anzeru pamafalitsa nzeru, koma mitima ya zitsiru siitero. Nsembe ya anthu oipa mtima imamuipira Chauta, koma pemphero la anthu olungama limamkondweretsa. Zochita za anthu oipa zimamnyansa Chauta, koma wochita zachilungamo Chauta amamkonda. Amene amasiya njira yabwino adzalangidwa koopsa. Amene amadana ndi kudzudzula adzafa. Manda ndi chiwonongeko ndi zosabisika kwa Mulungu, nanji tsono mitima ya anthu! Wonyada sakonda kumdzudzula, sapitako kwa anthu anzeru. Mtima wosangalala umaonetsa nkhope yachimwemwe, koma mtima wachisoni umaphwanya moyo. Mtima wa munthu womvetsa zinthu umafunitsitsa ndithu kudziŵa zambiri, koma m'kamwa mwa anthu opusa zauchitsiru zili pha! Munthu wozunzika masiku ake onse amakhala oipa, koma mtima wachimwemwe umakhala pa chisangalalo nthaŵi zonse. Kuli bwino kukhala ndi zinthu pang'ono nkumaopa Chauta, kupambana kukhala ndi chuma chambiri nkupeza nacho mavuto. Kuli bwino kudyera masamba pali chikondi, kupambana kudyera nyama ya ng'ombe yonenepa pali chidani. Munthu wopsa mtima msanga amautsa mkangano, koma munthu woleza mtima amabweretsa mtendere. Njira ya munthu waulesi ndi yoŵirira ndi minga, koma njira ya munthu wolungama imakhala ngati mseu wosalala. Mwana wanzeru amakondweretsa atate ake, koma mwana wopusa amanyoza amai ake. Uchitsiru umakondweretsa munthu wopanda nzeru, koma munthu womvetsa zinthu amatsata zolungama. Popanda uphungu zolinga zako zimalakwika, koma aphungu akachuluka, zolinga zako zimathekadi. Kuyankha mokhoza kumakondwetsa munthu, ndipo mau onena pa nthaŵi yake amakoma. Njira yopita ku moyo imakamufikitsa ku ntchito zangwiro, kuti alewe malo a anthu akufa kunsiko. Chauta amapasula nyumba ya munthu wonyada, koma amasamalira kadziko ka mkazi wamasiye. Maganizo a anthu oipa amamnyansa Chauta, koma mau a anthu olungama amamkondweretsa. Munthu wofunafuna phindu monyenga amavutitsa banja lake, koma munthu wodana ndi ziphuphu adzapeza bwino. Munthu wabwino amaganizira za m'mene ayankhire, koma pakamwa pa munthu woipa pamatuluka mau oipa okhaokha. Chauta amakhala kutali ndi anthu oipa mtima, koma amamva pemphero la anthu achilungamo. Maso okondwa amasangalatsa mtima, ndipo uthenga wabwino umalimbitsa munthu. Amene makutu ake amalandira bwino kudzudzula koyenera, adzakhala m'gulu la anthu anzeru. Munthu wonyoza malangizo amangodzinyoza yekha, koma wovomera kudzudzula amapindula nzeru yomvetsa zinthu. Kuwopa Chauta kumaphunzitsa nzeru, ndipo ndi kudzichepetsa ndi ulemu, chili patsogolo nkudzichepetsa. Zolinga zamumtima ndi za munthu, koma zolankhula zake ndi zochokera kwa Chauta. Ntchito zake za munthu zimakhala zolungama pamaso pake, koma Chauta amaweruza zamumtima. Uike ntchito zako m'manja mwa Chauta, ndipo zolinga zako zidzachitikadi. Chauta adapanga chinthu chilichonse kuti chikhale ndi cholinga chake, ngakhale anthu oipa, kuti aone tsiku la mavuto. Munthu aliyense wodzikuza amanyansa Chauta, ndithu ameneyo sadzalephera kulangidwa. Chifukwa cha kudzipereka ndi kukhulupirika, munthu amakhululukidwa machimo ake. Chifukwa choopa Chauta munthu amalewa zoipa. Pamene makhalidwe a munthu akondweretsa Chauta, ngakhale adani ake omwe amakhala naye mwamtendere. Kuli bwino kukhala ndi zinthu pang'ono uli ndi chilungamo kupambana kukhala ndi chuma chambirimbiri ulibe chilungamo. Mtima wa munthu umalingalira zoti uchite, koma Chauta ndiye amene amaongolera mayendedwe a munthuyo. M'kamwa mwa mfumu mumatuluka chigamulo chochokera kwa Mulungu. Pakamwa pa mfumu sipalakwa pogamula mlandu. Ndi Chauta amene amafuna kuti miyeso ndi masikelo zikhale zachilungamo. Miyala yonse yoyesera yam'thumba adaipanga ndi Chauta. Kuchita zoipa kumanyansa mafumu, pakuti chilungamo ndiye maziko a ufumu wao. Mau oona amakondweretsa mfumu, ndipo imamkonda munthu wolankhula chilungamo. Mfumu ikakwiya, ndiye kuti imfa ili pafupi, koma munthu wanzeru amaupepesa mkwiyowo. Kukoma mtima kwa mfumu kumadzetsa moyo, kuli ngati mitambo ya mvula yam'chilimwe. Kupata nzeru kumapambana kupata golide. Kumvetsa zinthu nkwabwino, kumapambana kukhala ndi siliva. Mseu wa munthu wolungama umapewa zoipa. Munthu wopenyetsetsa kumene akupita amasunga moyo wake. Kunyada kumafikitsa ku chiwonongeko, ndipo munthu wa mtima wodzikuza adzagwa. Kuli bwino kukhala ndi mtima wodzichepetsa pakati pa anthu osauka, kupambana kumagaŵana chuma ndi anthu onyada. Munthu wovomera malangizo, zinthu zidzamuyendera bwino, ndi wodala amene amadalira Chauta. Wa mtima wanzeru amamutcha wozindikira bwino zinthu, kulankhula kwake kokometsera kumakulitsa mphamvu ya mau ake. Nzeru ndi kasupe wopatsa moyo kwa amene ali nazo, koma uchitsiru umabweretsa chilango kwa anthu opusa. Mtima wa munthu wanzeru umamlankhulitsa mau ochenjera, nzeruzo zimakulitsa mphamvu ya mau ake. Mau okometsera ali ngati chisa cha uchi, amakoma mu mtima ndipo amalimbitsa thupi. Pamakhala njira ina yooneka yowongoka kwa munthu, koma kumapeto kwake imakhala njira ya ku imfa. Njala ya munthu wantchito imamthandiza kulimbikira, ndi njalayo imene imamkakamiza kuchita kanthu. Munthu wopandapake amakonzekera kuchita zoipa, mau ake ali ngati moto wopsereza. Munthu woipa mtima amafalitsa mkangano, kazitape amadanitsa anthu okhala pa chibwenzibwenzi. Munthu wandeu amakopa mnzake, ndipo amamuyendetsa m'njira yoipa. Amene amatsinzinira masoŵa, amalingalira zinthu zokhota, amene amachita msunamo amadzetsa zoipa. Imvi zili ngati chisoti chaufumu chopatsa ulemerero, munthu amazipata akakhala ndi moyo wautali. Munthu wosapsa mtima msanga amapambana wankhondo, amene amadzigwira mtima amapambana msilikali wogonjetsa mzinda. Maere amaŵaponya m'funkha, koma amene amaulula ndi Chauta. Kuli bwino kudya mkute wouma pali bata, kuposa kuchita madyerero m'nyumba m'mene muli mikangano. Kapolo wochita zinthu mwanzeru adzalamula mwana wa mfulu wochita zamanyazi, kapoloyo adzagaŵana nawo choloŵa ngati mmodzi mwa abale. Siliva amamuyesera m'chitofu, golide amamuyesera m'ng'anjo, koma mitima amaiyesa ndi Chauta. Wochita zoipa amamvera malangizo oipa, wabodza amamvera zochoka m'kamwa monyenga. Amene amalalatira mmphaŵi, amanyoza Mlengi wake. Amene amakondwerera tsoka la mnzake adzalangidwa. Zidzukulu ndiye ulemu wa anthu okalamba, ulemerero wa ana ndi atate ao. Kulankhula kwabwino sikuyenerana ndi chitsiru. Nanji kulankhula kwabodza, kodi kungayenerane ndi mfumu? Chiphuphu chili ngati mankhwala amwai kwa wochiperekayo, kulikonse kumene amapita, amalemera. Wokhululukira cholakwa amafunafuna chikondi, koma wosunga nkhani kukhosi amapha chibwenzi. Munthu wanzeru amamva kamodzi, munthu wopanda nzeru ndi samvamkunkhu. Munthu woipa mtima amangofuna zoukira. Tsono adzamtumira wamthenga wankhalwe. Kuli bwino kukumana ndi chimbalangondo cholandidwa ana, kupambana kukumana ndi chitsiru mu uchitsiru wake. Munthu akamabwezera zoipa kwa zabwino, tsoka silidzachoka pabanja pake. Chiyambi cha mkangano chili ngati kukhamulira madzi, ndiye uzichokapo ndeu isanabuke. Woweruza munthu woipa mtima kuti ndi wosalakwa, amanyansa Chauta, nayenso wopasa mlandu munthu wosalakwa amaipira Chauta. M'manja mwa wopusa mungakhalirenji ndalama zogulira nzeru, chikhalirecho mutu wake suyenda bwino? Bwenzi lako ndiye amakukonda nthaŵi zonse, ndipo mbale wako adabadwira kuti azikuthandiza pa mavuto. Munthu wopanda nzeru amapereka chikole, ndipo amasanduka chigwiriro pamaso pa mnzake. Wokonda zolakwa amakonda mkangano. Wokonda kulankhula zonyada amadziitanira chiwonongeko. Munthu wa mtima woipa zake sizimuyendera bwino. Ndipo wa pakamwa ponena zoipa amagwa m'tsoka. Mwana wopusa amamvetsa chisoni atate ake, bambo wake wa chitsiru sakhala ndi chimwemwe. Mtima wosangalala umakhala ngati mankhwala abwino, koma mtima woziya umaumitsa thupi. Munthu woipa amalandira chiphuphu cham'seri, ndipo amapotoza chigamulo cha mlandu. Munthu wanzeru amaika mtima pa nzeru, koma chitsiru chimangoti maso mwalamwala pa dziko lonse. Mwana wopusa amamvetsa chisoni atate ake, ndipo amapweteka mtima wa amai ake amene adambala. Kulipitsa munthu wosalakwa nkoipa. Si chilungamo kukwapula anthu abwino. Munthu wosunga pakamwa ndiye wodziŵa zinthu, munthu wodekha mtima ndiye womvetsa zinthu. Nchitsiru chomwe chikakhala chete, chimakhala ngati munthu wanzeru. Chikasunga pakamwa chimakhala ngati munthu wochenjera. Munthu wodzipatula mwa anzake amangotsata zomkomera iyeyo, amangofuna kutsutsana ndi zimene onse akudziŵa kuti ndi zoona. Chitsiru sichisamalako za kumvetsa zinthu. Koma chimangolankhula za maganizo ake okha. Kuipa mtima kukaoneka, pamabweranso manyozo, kunyozeka kumaitana manyazi. Mau a munthu angathe kukhala kasupe wa nzeru, ozama ngati nyanja yamchere yaikulu, omweka ngati a mu mtsinje wothamanga. Si kwabwino pa mlandu kukondera munthu woipa, kapena kupondereza munthu wosalakwa. Mau a chitsiru amautsa mkangano, ndipo pakamwa pake pamaitana mkwapulo. Pakamwa pa chitsiru ndipo pamabweretsa chiwonongeko chake. Mau ake ali ngati msampha wodzikolera mwiniwakeyo. Mau a kazitape ali ngati chakudya chokoma, anthu amaŵameza onse mokondwa. Wogwira ntchito yake mwaulesi, ali pachibale ndi munthu woononga zinthu. Chauta ali ngati nsanja yolimba, munthu wokhulupirira amathaŵiramo napulumuka. Chuma cha munthu wolemera chili ngati mzinda wake wolimba, chili ngati linga lalitali limene amayesa ndi lomutchinjiriza. Chiwonongeko chisanafike, mtima wa munthu umadzikuza, koma ulemu umatsatira kudzichepetsa. Ukayankha usanamve nkhani yonse, umaoneka wopusa ndipo umachita manyazi. Mtima wa munthu umatha kupirira matenda, koma munthu akataya mtima, ndani angathe kumlimbitsanso? Munthu wochenjera amafuna kuphunzirabe zambiri, amafunitsitsa kudziŵa bwino zinthu. Mphatso ya munthu imakhala ngati konza kapansi, imatha kumfikitsa pamaso pa akuluakulu. Amene amayamba kufotokoza mlandu wake amaoneka ngati wokhoza ndiye, mpaka mnzake atabwera nadzamufunsitsa bwino. Maere amathetsa mikangano. Amalekanitsa okangana amphamvu. Mnzako ukamthandiza amakhala ngati mzinda wolimba, koma kukangana naye kumakutsekera thandizo lililonse. Munthu amapeza bwino kapena ai, malinga ndi zolankhula zake, amalandira zotsatira za mau a pakamwa pake. Zimene umanena zingathe kukuphetsa kapena kukukhalitsa moyo, munthu wolankhulalankhula adzapeza bwino kapena tsoka. Wopeza mkazi, wapeza chinthu chabwino, Chauta wamukomera mtima. Anthu osauka amapemba, koma anthu olemera amayankha mwaukali. Pali abwenzi ena amene chibwenzi chao nchachiphamaso chabe, koma pali ena amene amakukangamira koposa mbale yemwe. Wosauka amene amayenda molungama amaposa munthu wopusa wolankhula zokhota. Si bwino kuti munthu akhale wosadziŵa zinthu, ndipo munthu woyenda mofulumira dziŵi amasokera. Kupusa kwake kwa munthu kukamgwetsa m'chiwonongeko, mtima wake umadzakwiyira Chauta. Chuma chimachulukitsa abwenzi atsopano, koma wosauka abwenzi ake amamthaŵa. Mboni yonama sidzalephera kulangidwa, wolankhula mabodza sadzapulumuka. Ambiri amafuna kuti munthu wopata aŵakomere mtima, munthu wooloŵa manja amakhala bwenzi la anthu onse. Ngati munthu wosauka abale ake omwe amadana naye, nanji abwenzi ake tsono! Iwo ndiye adzamthaŵira kunka kutali. Amayesetsa kuŵalondola mopembedzera, koma osaŵathanso. Amene amakonda nzeru amadzichitira zabwino mwiniwakeyo. Amene ali womvetsa, zinthu zidzamuyendera bwino. Mboni yonama sidzalephera kulangidwa, wolankhula mabodza adzaonongeka. Nkosayenera kuti chitsiru chizikhala ndi moyo wachuma, nanjinso kuti kapolo azilamulira akalonga! Nzeru zimapatsa munthu mtima wosakwiya msanga, ulemerero wake wagona pa kusalabadako za chipongwe. Mkwiyo wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango, koma kukoma mtima kwake kuli ngati mame pa udzu. Mwana wopusa ndi tsoka kwa atate ake, mkazi wolongolola ndi wotopetsa ngati mvula ya mvumbi. Nyumba ndi chuma ndiye choloŵa chochokera kwa makolo, koma mkazi wanzeru ndi wochokera kwa Chauta. Ulesi umagonetsa tulo tofa nato, choncho munthu waulesi adzavutika ndi njala. Munthu womvera malamulo amadzisungira moyo, koma munthu wonyoza malangizo a Mulungu adzafa. Wokomera mtima anthu osauka amachita ngati wokongoza Chauta, ndipo ndi Chautayo amene adzambwezera chifukwa cha ntchito zake. Uzimlanga mwana wako chikhulupiriro chikadalipo, ukapanda kutero, wamuwononga. Munthu wa ukali woopsa adzalandira chilango chomuyenerera, pakuti ukamlekerera wotereyu, zidzaipa koposa kale. Uzimvera malangizo ndi kuvomera mwambo, kuti ukhale ndi nzeru m'tsogolo. Munthu mumtima mwake amakonzekera zambiri, koma cholinga cha Chauta ndiye chimene chidzachitike. Chofunika kwa munthu nkukhulupirika. Kukhala wosauka nkwabwino koposa kukhala wonama. Kuwopa Chauta kumabweretsa moyo, ndipo amene amaopayo amakhala pabwino, ndiye kuti choipa sichidzamgwera. Waulesi amati akapisa dzanja m'mbale, kumamtopetsa kuti alifikitse kukamwa kwake. Ukamenya munthu wonyoza anzake, adzachenjererapo. Ukadzudzula munthu womvetsa bwino zinthu, adzapindulapo nzeru. Amene amachita ndeu ndi atate ake ndi kupirikitsa amai ake, ameneyo ndi mwana wochititsa manyazi ndiponso wonyozetsa. Mwana wanga, ukaleka kumvera malangizo, udzapatukana ndi mau opatsa nzeru. Mboni yachabe imanyoza chilungamo, pakamwa pa anthu oipa pamalikwira tchimo. Zakonzeka kale kuti mlandu uŵagwere anthu onyoza, mkwapulo ndi wokonzakonza kuti akwapulire pamsana pa zitsiru. Anthu okhuta vinyo amanyodola anzao, omwa zaukali amautsa phokoso. Aliyense wosokera nazo zimenezi ndi wopanda nzeru. Mkwiyo woopsa wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango. Amene amauputa dala mkwiyowo, amataya moyo wake. Nchaulemu kwa munthu kumalewa mikangano, koma aliyense wopusa amakonda kulongolola. Waulesi sasoseratu pa nthaŵi yoyenera. Pa nthaŵi yokolola adzafunafuna dzinthu, koma sadzapeza kanthu. Zolinga za mtima wa munthu zili ngati madzi ozama, ndi munthu wanzeru yekha angazitulutse. Anthu ambiri amalankhula za kukhulupirika kwao, koma ndani angathe kumpeza munthu wokhulupirika kwenikweni? Munthu abwino amakhala mwachilungamo, ndipo Mulungu amadalitsa ana amene amatsata njira yake. Pamene mfumu ikhala pa mpando wake wa chiweruzo, imazindikira ndi maso chabe anthu onse amene ali oipa. Ndani angathe kunena kuti, “Ine ndauyeretsa mtima wanga, ndilibenso tchimo lililonse.” Masikelo ndi miyeso ina yoyesera zinthu zikakhala zonyenga, zonsezo zimamunyansa Chauta. Ngakhale mwana yemwe amadziŵika ndi ntchito zake, kuti zimene amachitazo ndi zabwino ndi zolungama. Makutu amene timamvera ndiponso maso amene timapenyera, zonsezo adazilenga ndi Chauta. Usakondetse tulo, kuwopa kuti ungagwe mu umphaŵi. Khala maso, ndipo udzakhala ndi chakudya chambiri. Munthu akamagula kumene chinthu amati, “Nchoipa, nchoipa,” koma atagula nkuchokapo, amayamba kudzitama. Pali golide ndi miyala yambirimbiri yamtengowapatali, koma mau olankhula zanzeru ali ndi mtengo woposa zonsezo. Munthu amene waperekera mlendo chikole, umlande chovala chake, chimenecho chikhale chigwiriro chako, chifukwa chakuti waperekera chikole mlendo wosadziŵika. Chakudya chochipeza monyenga chimamkomera munthu, koma pambuyo pake chimakasanduka ngati lubwe m'kamwa mwake. Ukakonzekera kuchita zinthu, uziyamba wafunsa. Usanamenye nkhondo, uyambe wapempha malangizo oyenera. Amene amanka nachita ugogodi, amaulula zinsinsi. Nchifukwa chake usamagwirizane naye wolankhula zopusayo. Wina akatemberera bambo wake kapena mai wake, moyo wake udzatha ngati nyale yozima mu mdima wandiweyani. Choloŵa chopata mofulumira poyamba, sichidzakhala dalitso pambuyo pake. Usamanena kuti, “Ndidzabwezera choipa ndine.” Udikire Chauta, ndipo adzakuthandiza. Miyeso yosintha imanyansa Chauta, masikelo onyenga ndi oipanso. Mayendedwe a munthu amaŵalamula ndi Chauta: Tsono munthu angadziŵe bwanji njira yake? Ndi msampha kwa munthu kupereka chinthu kwa Chauta mosaganiza bwino, chifukwa mwina atha kusintha maganizo atalumbira kale. Mfumu yanzeru imazindikira oipa, ndipo imaŵalanga mopanda chisoni. Mpweya wa munthu uli ngati nyale ya Chauta, nyaleyo imafufuza ziwalo zake zonse zam'kati. Kukoma mtima ndi kukhulupirika ndizo zimasunga mfumu, chilungamo ndiye chimalimbitsa ufumu wake. Kukongola kwa achinyamata kwagona pa nyonga zao, koma ulemerero wa nkhalamba wagona pa imvi zao. Mikwingwirima ndiye mankhwala ochotsa zoipa. Mikwapulo imachiza zam'katikati mwa munthu. Mtima wa mfumu uli ngati mtsinje wa madzi m'manja mwa Chauta. Amauwongolera ku zimene Iyeyo akufuna. Makhalidwe a munthu amakhala olungama pamaso pa mwiniwakeyo, koma Chauta ndiye amayesa mtima wake. Kuchita zolungama ndi zokhulupirika kumakondweretsa Chauta koposa kupereka nsembe. Maso odzikuza ndi mtima wonyada zimatsogolera anthu oipa ngati nyale, nchifukwa chake amachimwa. Zolinga za munthu wakhama zimachulukitsa dzinthu dzake, koma aliyense wochita zinthu mofulumira udyo, amangokhala wosoŵa. Chuma chomachipeza monyenga chimangoti wuzi ngati nthunzi, ndipo chimakola anthu mu msampha wa imfa. Ndeu za anthu oipa zidzaŵaononga, poti amakana kuchita zolungama. Njira ya munthu woipa ndi yokhotakhota, koma khalidwe la munthu wosachimwa ndi lolungama. Kuli bwino kukhala potero pa denga kupambana kukhala m'nyumba pamodzi ndi mkazi wolongolola. Mtima wa munthu woipa umalakalaka zoipa. Samva chifundo konse ndi mnzake wovutika. Munthu wonyoza akalangidwa, wopusapusa amaphunzirapo nzeru. Munthu wanzeru akamlangiza, amamvetsa zambiri. Mulungu ngwachilungamo nthaŵi zonse, amadziŵa zimene anthu oipa akuchita ndipo adzawaononga. Amene amatseka m'khutu wosauka akamalira, adzalira iyenso, koma kulira kwakeko sikudzamveka. Mphatso yam'seri imaposa ukali, ndipo chiphuphu chosereza chimathetsa mphamvu ngakhale ya mkwiyo woopsa. Chilungamo chikachitika, nzika zabwino zimakondwera, koma zimadederetsa atambwali. Munthu amene amasiya njira ya anthu anzeru, adzapezeka m'gulu la anthu akufa. Amene amakondetsa zosangalatsa, adzasanduka munthu wosauka. Amene amakondetsa vinyo ndi mafuta, sadzalemera. Oipa adzakhala choombolera anthu abwino, ndipo osakhulupirika adzakhala choombolera anthu a mtima wabwino. Kuli bwino kukhala ku chipululu kupambana kukhala ndi mkazi wolongolola ndi wopsa mtima msanga. Munthu wanzeru samwaza chuma chake, koma munthu wopusa amachiwononga. Amene amatsata chilungamo ndi chifundo adzapeza moyo ndi ulemu. Munthu wanzeru amagonjetsa mzinda wa anthu a mphamvu, ndipo amagwetsa linga lamphamvu limene anthuwo ankalikhulupirira. Amene amagwira pakamwa ndi kusamala zokamba zake, sapeza mavuto. Munthu wonyada ndi wodzikuza amamtchula “Mnyodoli,” chifukwa amachita zinthu modzitama ndi mwachipongwe. Kulakalaka kwa munthu waulesi kumamupha, poti amangokhala manja ali khoba, osagwira ntchito. Tsiku lathunthu anthu oipa amasirira zinthu, koma omvera Mulungu amapatsa ndipo alibe kaliwumira. Nsembe ya anthu oipa imamnyansa Chauta, nanji tsono akaipereka ndi cholinga choipa! Mboni yonama idzaonongeka, koma mau a munthu wakumva adzamveka nthaŵi zonse. Munthu woipa amafuna kuwoneka wolimba mtima, koma munthu woongoka amaganizira bwino zochita zake. Palibe nzeru, palibe kumvetsa zinthu, palibe ngakhale uphungu, zimene zingathe kupambana Chauta. Kavalo amamkonzera tsiku la nkhondo, koma ndi Chauta amene amapambanitsa. Mbiri yabwino ndi yofunika kupambana chuma chambiri, kupeza kuyanja nkopambana siliva ndi golide. Wolemera ndi wosauka akulingana, pakuti onsewo adaŵalenga ndi Chauta. Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala, koma wopusa amangopitirira ndipo amanong'oneza bondo. Mphotho ya munthu wodzichepetsa ndi woopa Chauta, ndi chuma, ulemu ndi moyo. M'njira ya munthu wosalungama muli minga ndi misampha, koma wodzisamala bwino adzazilewa zonsezo. Mwana muzimuphunzitsa njira yoti aziyendamo, ndipo atakalamba sadzachokamo m'njira imeneyo. Wolemera amalamulira wosauka, ndipo wokongola zinthu amakhala kapolo wa womkongozayo. Amene amabzala kusalungama adzakolola mavuto, ndipo ndodo ya ukali wake idzathyoka. Amene ali ndi diso lachifundo adzadalitsidwa, poti amagaŵana chakudya chake ndi anthu osauka. Mukampirikitsa wonyoza, kukangana kudzatha, ndipo ndeu ndi zonyoza zidzalekeka. Amene amakonda kukhala woyera mtima ndi kulankhula zabwino, adzakhala bwenzi la mfumu. Chauta amayang'anira bwino anthu odziŵa zinthu, koma mau a anthu osakhulupirika, Iye amaŵalepheretsa. Waulesi amati, “Pali mkango pabwalopo! Ndikaphedwa m'miseu.” Pakamwa pa mkazi wachigololo pali ngati dzenje lakuya. Amene Chauta amamkwiyira adzagwamo. Kupusa kumakhala mumtima mwa mwana, koma ndodo yomlangira mwanayo idzachotsa kupusako. Amene amapondereza osauka kuti aonjezere pa chuma chake, kapena amene amangopatsa zinthu olemera okha, adzasanduka wosauka. Utchere khutu lako, umve mau a anthu anzeru, uike mtima wako pa zophunzitsa zanga, kuti uzidziŵe. Chidzakhala chokondwetsa ukazisunga, ndi kukhala wokonzeka kumazilankhula pa nthaŵi yake. Ndakudziŵitsa zimenezi lero kuti makamaka iweyo uzikhulupirira Chauta. Kodi suja ndidakulembera malangizo makumi atatu, okuchenjeza ndi okupatsa nzeru, malangizo okudziŵitsa zolungama ndi zoona, kuti ukaŵayankhe zoona amene adakutuma? Mmphaŵi usamubere, chifukwa choti iyeyo ndi wosauka. Anthu ozunzika usaŵapondereze pa bwalo la milandu. Pakuti Chauta adzaŵateteza pa mlandu wao, ndipo adzaŵalanda moyo amene amalanda zinthu zao. Usachite naye chibwenzi munthu wopsa mtima msanga, ndipo usamayenda naye munthu waukali, kuwopa kuti ungadzaphunzireko mayendedwe ake, ndi kukodwa mu msampha. Usakhale mmodzi mwa anthu opereka zikole, amene amasanduka chigwiriro cha ngongole. Ngati ulephera kulipira, adzakulanda ngakhale bedi lako lomwe. Usasendeze malire akalekale amene makolo ako adaŵaika. Kodi ukumuwona munthu wochita ntchito zake mwaluso? Iye adzatumikira mafumu, sadzatumikira anthu wamba. Ukakhala pansi kuti udye ndi mfumu, uyang'ane bwino zimene zili pamaso pako. Ngati ndiwe munthu wadyera, udziletse kuti usachite khwinthi. Usasirire zakudya zake zokoma, poti zimenezi ndi zakudya zonyenga. Usadzitopetse nkufuna chuma, udziŵe kuchita zinthu mwanzeru ndi kudziletsa. Ukangopeza chuma, uwona chapita kale, pakuti chimachita ngati chamera mapiko mwadzidzidzi, nkuyamba kuuluka kunka kumwamba ngati chiwombankhanga. Usadye chakudya kwa munthu waunkhambo, usamalakalaka zakudya zake zokoma. Paja iye amangokhalira kuganiza za mtengo wa zinthu. Amakuuza kuti, “Kazidya, kazimwa!” Koma mumtima mwake zimenezo sakuzifuna. Udzasanza nthongo wadyazo, ndipo mau ako oshashalika adzapita pachabe. Usamalankhula pali munthu wopusa, pakuti adzanyoza mau ako anzeru. Usasendeza malire akalekale, kapena kukaloŵerera minda ya ana amasiye. Paja Momboli wao ndi wamphamvu, adzaŵateteza pa mlandu wao kuti akutsutse iweyo. Mtima wako ukhale pa malangizo, ndipo makutu ako azimvetsera mau anzeru. Usamaleka kumpatsa mwambo mwana, ukamkwapula ndi tsatsa sadzafa. Ngati umkwapula ndi tsatsa, udzapulumutsa moyo wake ku imfa. Mwana wanga, mtima wako ukakhala wanzeru, nanenso mtima wanga udzasangalala. Mtima wanga udzakondwa ndikadzakumva ukulankhula zolungama. Mtima wako usamachita nsanje ndi anthu ochimwa, koma upitirire kumaopa Chauta tsiku ndi tsiku. Ndithu, zakutsogolo zilipo, ndipo chikhulupiriro chako sichidzakhala chachabe. Mwana wanga, tamvera, ndipo ukhale wanzeru, mtima wako uuyendetse m'njira yabwino. Usakhale pakati pa anthu amene amaledzera, kapena pakati pa anthu odya nyama mwadyera. Paja chidakwa ndi munthu wadyera adzasanduka amphaŵi, ndipo munthu waulesi adzasanduka mvalansanza. Umvere atate ako amene adakubala, ndipo usamanyoza amai ako atakalamba. Ugule choona, ndipo usachigulitse. Ugulenso nzeru, mwambo ndiponso mtima womvetsa zinthu. Bambo wa mwana waulemu adzakondwa kwambiri. Wobala mwana wanzeru adzasangalala naye. Atate ako ndi amai ako asangalale, mai amene adakubala iwe akondwe. Mwana wanga, mtima wako ukhulupirire ine, maso ako apenyetsetse njira zanga. Mkazi wadama ali ngati dzenje lakuya, mkazi wachiwerewere ali ngati chitsime chophaphatiza. Amabisalira ngati mbala yachifwamba, ndipo chifukwa cha iyeyo amuna ambiri amasanduka osakhulupirika. Ndani ali ndi tsoka? Ndani ali ndi chisoni? Ndani ali pa mkangano? Ndani akudandaula? Ndani ali ndi zilonda zosadziŵika magwero ake? Ndani ali wofiira maso? Ndi amene amakhalitsa pamene pali vinyo, amene amamwa nawo vinyo wosanganiza ndi zina. Usatengeke mtima ndi kufiira kwa vinyo, pamene akututuma m'chikho namakoma poloŵa ku m'mero. Potsiriza pake amaluma ngati njoka, ndipo amanjenjedula ngati mphiri. Maso ako adzaona zinthu zachilendo, maganizo ndi mau ako adzakhala okhotakhota. Udzakhala ngati munthu amene ali gone pakati pa nyanja, kapena ngati munthu wogona pa nsonga ya mlongoti wa ngalaŵa. Iwe udzati, “Adanditchaya, koma sadandipweteke. Adandimenya, koma ine osamvako. Kodi ine ndidzatsitsimuka liti? Ndiye ndithamangira chakumwa china.” Usamachitira nsanje anthu ochimwa, kapena kumalakalaka kuti uzimvana nawo, chifukwa mitima yao imalingalira zandeu, ndipo pakamwa pao pamalankhula zoutsa mavuto. Nyumba imamangidwa ndi anthu anzeru, ndipo imakhazikika ndi anthu a mtima wodziŵa zinthu. Wodziŵa zinthu angathe kudzaza zipinda zake ndi chuma chokondweretsa ndi cha mtengo wapatali. Munthu wanzeru ndi wamphamvu kupambana munthu wa nyonga zambiri, munthu wophunzira amaposa munthu wamphamvu. Pafunika malangizo abwino kuti ukamenye nkhondo. Aphungu akachuluka, kupambana kuli pomwepo. Nzeru ndi yapatali kwambiri kwa munthu wopusa, alibe chonena pa bwalo lamilandu. Amene amakonzekera kuchita choipa, adzatchedwa mvundulamadzi. Kukonzekera zopusa nkuchimwa, munthu wonyoza amanyansa anthu. Ukataya mtima pamene upeza zovuta, ndiye kuti mphamvu zako ndi zochepa. Uŵapulumutse amene akutengedwa kuti akaphedwe. Uŵalanditse amene akuyenda movutikira popita kukaŵapha. Ukanena kuti, “Ife sitidazidziŵe zimenezi,” kodi iye amene amayesa mtima, zimenezi saziwona? Kodi amene amayang'anira moyo wako sazidziŵa? Kodi sadzambwezera munthu potsata ntchito zake? Mwana wanga, uzidya uchi poti ndi wabwino, madzi a m'chisa cha njuchi ndi ozuna ukaŵalaŵa. Udziŵe kuti nzeru ndi yoteronso mumtima mwako. Ukaipeza, zinthu zidzakuyendera bwino m'tsogolo, ndipo chikhulupiriro chako sichidzakhala chachabe. Nyumba ya munthu wabwino usaichite zachifwamba ngati munthu woipa mtima, usachite nayo nkhondo nyumba yake. Munthu wabwino amagwa kasanunkaŵiri, koma amadzukirira ndithu, m'menemo anthu oipa tsoka limaŵagwera chonse. Usamakondwerera kugwa kwa mdani wako, mtima wako usamasangalala iyeyo akaphunthwa. Ukatero Chauta adzaziwona zimenezo nadzaipidwa nazo, kenaka adzaleka kumkwiyira mdani wakoyo. Usamavutika chifukwa cha anthu ochita zoipa, usachite nawo nsanje anthu oipa. Pajatu munthu woipa zinthu sizidzamuyendera bwino m'tsogolo, moyo wa anthu oipa adzauzima ngati nyale. Mwana wanga, uziwopa Chauta ndiponso mfumu, usagwirizane ndi anthu okonda kuŵachitira mwano. Ameneŵa amatha kugwetsa tsoka mwadzidzidzi, ndani angadziŵe kuwopsa kwa chiwonongeko chochokera kwa aŵiriŵa? Enanso ndi aŵa malangizo a anthu anzeru: Kukondera pozenga milandu si chinthu chabwino. Amene amauza munthu woipa kuti, “Ndiwe wosalakwa,” anthu adzamtemberera, ndipo mitundu ya anthu idzaipidwa naye. Koma aweruzi amene amalanga anthu oipa adzapeza bwino, ndipo adzakhala ndi madalitso ambiri. Munthu woyankha zoona ndiye amaonetsa chibwenzi chenicheni. Ukonzeretu ntchito zako zonse makamaka zakumunda, pambuyo pake mpamene ungayambe kumanga nyumba. Usakhale mboni yotsutsa mnzako popanda chifukwa, pakamwa pako pasamanena zonama. Usamanena kuti, “Ndidzamchitira monga momwe iye wandichitira ine, ndidzamlipsira chifukwa cha zomwe iye wandichitira ine.” Ndinkayenda m'mbali mwa munda wa munthu waulesi, m'mbali mwa munda wamphesa wa munthu wopanda nzeru. M'minda monsemo munali mutamera minga yokhayokha, m'nthaka imeneyo munali mutamera khwisa, ndipo mpanda wake wamiyala unali utagwa. Tsono nditaona, ndidayamba kuganizirapo pa zimenezo, nditayang'ana, ndidatolapo phunziro ili: Ukati, “Taimani ndigoneko pang'ono,” kapena “Ndiwodzereko chabe,” kapena “Ndingopumulako pang'ono,” umphaŵi udzakufikira monga mbala, kusauka kudzakupeza ngati mbala yachifwamba. Enanso ndi aŵa malangizo a Solomoni amene anthu a Hezekiya, mfumu ya ku Yuda adaŵalemba: Ulemerero wa Mulungu wagona pa kubisa zinthu, m'menemo ulemerero wa mafumu wagona pa kuzifufuza zinthuzo. Monga momwe uliri mlengalenga kutalika, ndi momwe liliri dziko lapansi kuzama, ndi m'mene aliri maganizo a mfumu kusadziŵika kwake. Chotsa zoipa m'siliva, ndipo wosula adzatha kupanga naye chiŵiya. Muchotse aphungu oipa pamaso pa mfumu, ndipo ufumu wake udzakhazikika pa chilungamo. Usamadzikuza ukakhala pamaso pa mfumu, usamakhala pa malo a anthu apamwamba. Pajatu kuli bwino kuchita kukuuza kuti, “Dzakhale pokwera pano”, koposa kuchita kukutsitsa chifukwa cha wina wokupambana. Zimene maso ako azipenya, usafulumire kupita nazo ku bwalo lamilandu, chifukwa udzatani nanga pambuyo pake, ngati mnzako akuchititsa manyazi pokutsutsa? Mnzako uzichita kukamba naye zinthu, ndipo usaulule chinsinsi cha wina, kuwopa kuti wina akamva mau ako, angakuchititse manyazi, ndipo mbiri yako yoipa sidzatha. Mau amodzi olankhula moyenera ali ngati zokongoletsera zagolide m'choikamo chasiliva. Kwa munthu womvetsera bwino, kudzudzula kuli ngati mphete yagolide, kapena chokongoletsera china chagolide. Kwa anthu amene amtuma, wamthenga wokhulupirika ali ngati madzi ozizira pa nthaŵi yotentha, amaziziritsa mtima wa mbuyake. Munthu wonyadira mphatso imene saipereka, ali ngati mitambo ndi mphepo zopanda mvula. Kupirira ndiye kumagonjetsa wolamula, ndipo kufeŵa m'kamwa kumafatsitsa mtima wouma. Ukapeza uchi, ingodya wokukwanira, kuwopa kuti ungakoledwe nawo nkuyamba kusanza. Kunyumba kwa mnzako uzipitako kamodzikamodzi, kuwopa kuti angatope nawe, nkuyamba kudana nawe. Munthu wochitira mnzake umboni wonama, amapweteka mnzakeyo ngati chibonga kapena lupanga kapena muvi wakuthwa. Kukhulupirira munthu wosakhulupirika pa nthaŵi yamavuto kuli ngati kudya ndi dzino loŵaŵa, kapena kuyenda ndi mwendo wothyoka. Kuimbira nyimbo munthu wachisoni kuli ngati kumvula zovala pa nyengo yachisanu, ndiponso ngati kumthira vinyo wosasa pa chilonda. Mdani wako akakhala ndi njala, umpatse chakudya, akamva ludzu, umpatse madzi akumwa. Potero udzamchititsa manyazi aakulu, ndipo Chauta adzakupatsa mphotho. Mphepo ya mpoto ndiyo imadza ndi mvula, chonchonso mjedu umadzetsa mkwiyo. Kuli bwino kukhala potero pa denga, kupambana kukhala m'nyumba pamodzi ndi mkazi wolongolola. Mthenga wabwino wochokera ku dziko lakutali uli ngati madzi ozizira kwa munthu waludzu. Munthu wabwino amene amagonjera munthu woipa amafanafana ndi kasupe wodzaza ndi matope kapena chitsime cha madzi oipa. Si kwabwino kudya uchi wambiri, tsono muchenjere nawo mau oyamikira. Munthu wosadzimanga mtima ali ngati mzinda umene adani authyola nkuusiya wopanda malinga. Ulemu woulandira chitsiru uli ngati chisanu chambee chomagwa nthaŵi yachilimwe, kapena mvula yomagwa nthaŵi yokolola. Monga imachitira mpheta yokhalira kuuluka, monga amachitira namzeze kumangoti zwezwezwe, ndimonso limachitira temberero lopanda chifukwa, silitha. Mkwapulo ndi wokwapulira kavalo, chitsulo ncha m'kamwa mwa bulu, chonchonso ndodo ndi yoyenerera zitsiru. Chitsiru usamachiyankha potsata uchitsiru wake, kuwopa kuti ungafanefane nacho. Koma mwina uzichiyankha chitsiru potsata uchitsiru wake, kuwopa kuti chingamadziyese chanzeru. Amene amatuma chitsiru kukanena uthenga, amachita ngati kudzidula mapazi ndipo amadziitanira mavuto. Monga miyendo ya munthu wopunduka imakhala yopanda ntchito, ndimonso umakhalira mwambi m'kamwa mwa zitsiru. Amene amachitira chitsiru ulemu ali ngati munthu wokulunga mwala m'khwenengwe. Monga imachitira minga yobaya dzanja la chidakwa ndimonso umakhalira mwambi m'kamwa mwa zitsiru. Amene amalemba ntchito chitsiru chongodziyendera kapena chidakwa, ali ngati munthu woponya mivi amene amangolasa anthu chilaselase. Chitsiru chimene chimabwerezabwereza za uchitsiru wake chili ngati galu wodya masanzi ake omwe. Ngakhale chitsiru chomwe nkuti ndiponi, pali chikhulupiriro, koma osati munthu wodziyesa wanzeru pamene ali wopusa. Waulesi amati, “Pali mkango pa njira! Mumseumo muli mkango!” Monga chitseko chimatembenukira uku ndi uku pa zomangira zake, ndimonso waulesi amangokunkhulira pabedi pake. Waulesi amati akapisa dzanja lake m'mbale, kumamtopetsa kuti alifikitse kukamwa kwake. Waulesi amadziyesa wanzeru kupambana anthu asanu ndi aŵiri amene angathe kuyankha mochenjera. Amene angoloŵerera ndeu ya eniake, ali ngati munthu wombwandira galu wongodziyendera. Monga munthu wopenga amene amangoponya nsakali zamoto, kapena mivi yoopsa, ndimonso amakhalira munthu wonyenga mnzake, amene amati, “Ai, ndi zoseka chabe!” Moto umazima pakasoŵa nkhuni, chonchonso kumene kulibe kazitape, kulibenso ndeu. Monga momwe aliri makala pa moto wonyeka ndiponso nkhuni pa moto woyaka, ndimonso amakhalira munthu wandeu poutsa mikangano. Mau a kazitape ali ngati zakudya zokoma, zimene zimatsikira m'mimba msanga. Monga m'mene chiziro chimakutira chiŵiya chadothi, ndimonso mau oshashalika amabisira mtima woipa. Munthu wachidani pakamwa pake pamalankhula zabwino, pamene mumtima mwake muli zonyenga. Woteroyo akamalankhula mokometsa mau, usamkhulupirire, pakuti mumtima mwake mwadzaza zoipa. Ngakhale amabisa chidani mochenjera, kuipa kwakeko kudzaoneka poyera pakati pa anthu. Amene amakumba dzenje adzagwamo yekha, amene amakunkhuniza mwala, udzampsinja iye yemweyo. Munthu wonama amadana ndi amene iye adaŵapweteka, pakamwa poshashalika mpoononga. Usamanyadira zamaŵa, pakuti sudziŵa zimene zidzachitika pa tsikulo. Akutame ndi wina, osati pakamwa pako pomwe, wosadziŵana naye akakutamanda, apo ndipo. Mwala ndi wolemera, ndipo mchenganso ndi wolemera kwambiri, koma makani a chitsiru ndi oposa zonsezo kulemera kwake. Mkwiyo umadzetsa nkhanza, kupsa mtima kumachititsa zoopsa, koma nsanje imabweretsa zoipa zopambana. Kudzudzula munthu poyera nkwabwino kupambana kubisa chikondi chimene uli nacho. Amene amakukonda, ngakhale akupweteke, chikondi chake chimakhalapobe, mdani wako ngakhale akumpsompsone, nkunyenga chabe kumeneko. Wokhuta amaipidwa ndi chisa cha uchi, koma kwa munthu wanjala ndi zoŵaŵa zomwe zimatsekemera. Munthu amene wasokera kutali ndi kwao, ali ngati mbalame yosokera kutali ndi chisa chake. Mafuta ndi zonunkhira zimasangalatsa mtima, koma kukoma kwa bwenzi kwagona pa malangizo ake. Usasiye bwenzi lako ndiponso bwenzi la atate ako. Usachite kupita ku nyumba ya mbale wake, ukakhala pa mavuto. Mnzako wokhala naye pafupi amaposa mbale wako wokhala kutali. Mwana wanga, ukhale ndi nzeru, ukondwetse mtima wanga, kuti choncho ndithe kumuyankha amene amandinyoza. Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala, koma wopusa amangopitirira ndipo amanong'oneza bondo. Munthu amene waperekera mlendo chikole, umlande chovala chake, chimenecho chikhale chigwiriro chako, chifukwa chakuti waperekera chikole mlendo wosadziŵika. Wopatsa mnzake moni mofuula m'mamaŵa kwambiri, adzamuyesa kuti akutemberera. Mkazi wolongolola ndi wotopetsa ngati mvula ya mvumbi. Kuyesa kumletsa mkazi woteroyo kuli ngati kuyesa kuletsa mphepo, kapena kuyesa kufumbata mafuta m'manja. Chitsulo amachinola nchitsulo chinzake, chonchonso munthu amasulidwa ndi munthu mnzake. Amene amasamalira mkuyu adzadya zipatso zake, chonchonso amene amasamalira mbuyake adzalandira ulemu. Monga momwe nkhope imaonekera m'madzi, momwemonso mtima wa munthu umadziŵika ndi zochita zake. Manda sakhuta, nawonso maso a munthu sakhuta. Siliva amasungunulira mu uvuni, golide amasungunulira m'ng'anjo, chonchonso munthu amayesedwa ndi mbiri yake. Chitsiru ngakhale uchisinje mu mtondo ndi munsi pamodzi ndi chimanga, kupusa kwake sikudzachoka konse. Uzidziŵe bwino nkhosa zako m'mene ziliri, ndipo usamalire ziŵeto zako. Paja chuma sichikhala mpaka muyaya. Kodi ufumu umakafika mpaka ku mibadwo yonse? Udzu ukatha, msipu nkuphuka, ndipo atatuta udzu wakumapiri, anaankhosa adzakupatsa chovala, ndi ubweya wao, ndipo pogulitsa mbuzi udzapeza chogulira munda. Udzakhala ndi mkaka wambiri wa mbuzi kuti uzidya, iweyo ndi banja lako, ndiponso ndi adzakazi ako omwe. Woipa mtima amangodzithaŵira popanda wina wompirikitsa, koma wochita zabwino amalimba mtima ngati mkango. Eni dziko akachita zaupandu, oŵalamulira amachuluka. Koma anthu akakhala omvetsa ndi odziŵa zinthu, dzikolo limakhazikika nthaŵi yaitali. Munthu wosauka amene amapondereza osauka anzake, ali ngati mvula yamkuntho yosasiya konse chakudya m'minda. Amene samvera malamulo amatamanda anthu oipa mtima, koma otsata malamulo amatsutsana nawo. Anthu oipa samvetsa kuti chilungamo nchiyani, koma amene amatsata kufuna kwa Chauta amachimvetsa kwathunthu. Munthu wosauka amene amayenda mwaungwiro amaposa kwambiri munthu wolemera amene ali wonyenga. Amene amatsata malamulo ndiye mwana wanzeru, koma amene amayenda ndi anthu adyera, amachititsa atate ake manyazi. Amene amachulukitsa chuma chake polandira chiwongoladzanja ndi pochikundika, chumacho amachikundikira ena amene adzachitira chifundo anthu osauka. Wina akamakana kumvera malamulo, ngakhale mapemphero ake amanyansira Mulungu. Amene amasokeza anthu olungama kuti azitsata njira yoipa, adzagwa m'dzenje lake lomwe. Koma anthu amene alibe cholakwa adzalandira choloŵa chabwino. Munthu wolemera amadziyesa wanzeru, koma munthu wosauka amene ali womvetsa zinthu, amamtulukira. Anthu abwino akapambana, pamakhala chikondwerero chachikulu, koma oipa mtima akalandira ulamuliro, anthu amabisala. Wobisa machimo ake sadzaona mwai, koma woulula ndi kuleka machimo, adzalandira chifundo. Ndi wodala munthu amene amaopa Chauta nthaŵi zonse, koma woumitsa mtima wake adzagwa m'tsoka. Monga muja umakhalira mkango wobangula kapena chimbalangondo cholusa, ndimonso imakhalira mfumu yoipa mtima kwa anthu osauka. Wolamulira amene samvetsa zinthu amapondereza anthu mwankhanza, koma wodana ndi phindu loipa amatalikitsa masiku ake. Munthu amene wapalamula mlandu wopha mnzake, akhale womathaŵathaŵa mpaka kufa kwake. Wina aliyense asamthandize. Amene amayenda mokhulupirika adzapulumutsidwa, koma woyenda mokhotakhota adzagwa m'dzenje. Wolima m'munda mwake adzakhala ndi chakudya chambiri, koma wonka nafuna zopanda pake adzasauka kwambiri. Munthu wokhulupirika adzakhala ndi madalitso ambiri, koma wofunitsitsa kulemera msanga sadzalephera kupeza chilango. Kuchita tsankho si kwabwino, komabe ena amaweruza mokondera chifukwa cha kachidutswa ka buledi. Munthu wakaliwumira amafunitsitsa kulemera mofulumira, koma sadziŵa kuti umphaŵi udzamgwera. Amene amadzudzula mnzake, potsiriza pake mnzakeyo adzamkonda kwambiri kupambana amene ali ndi mau oshashalika. Wobera atate ake kapena amai ake namanena kuti kutero sikulakwa, ameneyo ndi mnzake wa munthu woononga. Munthu waumbombo amautsa mkangano, koma wokhulupirira Chauta adzalemera. Samvazaanzake nchitsiru, koma wotsata nzeru za ena adzapulumuka. Amene amapatsa osauka sadzasoŵa kanthu koma amene amatsinzina dala kuti asaŵapenye, adzatembereredwa kwambiri. Anthu oipa mtima akalandira ulamuliro, anthu amabisala, koma oipawo akaonongeka, anthu ochita chilungamo amapeza bwino. Munthu wochita liwuma kwina atamdzudzula, adzaonongeka mwadzidzidzi osachiranso. Mu dziko mukakhala chilungamo, anthu amakondwa, koma chilungamo chikasoŵa, anthu amadandaula. Wokonda nzeru amasangalatsa atate ake, koma amene amayenda ndi akazi adama amamwaza chuma chake. Mfumu imalimbitsa dziko pakuweruza molungama, koma imene imaumiriza anthu kuti aipatse ziphuphu, imaononga dziko. Munthu amene amathyasika mnzake amadzitchera msampha yekha. Munthu woipa amakodwa ndi zolakwa zake, koma wochita chilungamo amakhala wokondwa ndi womasuka. Munthu wokoma mtima amasamalira zoyenerera osauka, koma munthu woipa salabadako za zimenezo. Anthu onyoza akhoza kuyatsa mzinda, koma anthu anzeru amabweza ukali. Munthu wanzeru atatsutsana ndi chitsiru, chitsirucho chimangochita phokoso nkumaseka, ndipo sipakhala mtendere. Anthu okhetsa magazi amadana ndi munthu wosalakwa, koma anthu angwiro amateteza moyo wake. Wopusa amaonetsa mkwiyo wake, koma munthu wanzeru amadzigwira. Wolamula akamamvera zabodza, nduna zake zonse zidzakhala zoipa. Munthu wosauka ndi munthu wopondereza anzake amafanafana pa ichi, chakuti onsewo Chauta ndiye adaŵapatsa maso. Mfumu ikamaweruza osauka mosakondera, ufumu wake udzakhazikika mpaka muyaya. Mkwapulo ndi chidzudzulo zimapatsa nzeru, koma mwana womamlekerera amachititsa amake manyazi. Oipa akamalamulira, zolakwa zimachuluka, koma ochita chilungamo adzaona kugwa kwa oipawo. Uzimlanga mwana wako ndipo adzakupatsa mtendere mu mtima, adzakondweretsa mtima wako m'tsogolo. Kumene kulibe mithenga yochokera kwa Mulungu, anthu saweruzika, ndi wodala munthu amene amatsata malamulo. Munthu wotumikira samulanga ndi mau chabe, ngakhale aŵamvetse mauwo, sadzasamalako. Ngakhale chitsiru chomwe nkuti ndiponi pali chikhulupiriro, koma osati munthu wodziyesa wanzeru pamene ali wopusa. Amene amasasatitsa kapolo wake kuyambira ali mwana, pomaliza pake adzapeza kuti kapoloyo wasanduka mloŵachuma wake. Munthu wamangaŵa amautsa mikangano, munthu wokalipakalipa amabweretsa zolakwa zambiri. Kunyada kwa munthu kudzamtsitsa, koma amene ali wodzichepetsa adzalandira ulemu. Woyenda ndi mbala ndi wodana ndi moyo wake, amamva kutemberera, koma osaulula kanthu. Kuwopa anthu kuli ngati msampha, koma wodalira Chauta amakhala pabwino. Ambiri amafunitsitsa kuti wolamulira aŵakomere mtima, koma munthu amamuweruza molungama ndi Chauta yekha. Anthu osoŵa chilungamo amanyansa anthu ochita chilungamo, monga momwe anthu abwino amanyansira anthu oipa mtima. Naŵa mau a Aguri, mwana wa Yake, wa ku Masa: Inu Mulungu, ine ndatopa. Inu Mulungu, ine ndatopa, ndalefukiratu. Ndithudi, ine ndine wopusa koposa anthu onse. Ndilibe nzeru zonga za munthu. Sindidaphunzire nzeru, ndipo Woyera uja sindimdziŵa. Kodi ndani adaakwera kumwamba natsikako? Ndani adafumbatapo mphepo m'manja? Ndani adafukusapo madzi m'chovala? Ndani adakhazikitsa mathero onse a dziko lapansi? Dzina lake ndani, ndipo mwana wake dzina lake ndani? Tanenatu ngati ukudziŵa! Mau aliwonse a Mulungu ndi oona. Iye ndiye chishango choteteza amene amathaŵira kwa Iye. Pa mau ake usamaonjezeko kanthu, kuwopa kuti angakudzudzule, ndipo ungapezeke kuti ndiwe wabodza. Inu Mulungu, ndikukupemphani zinthu ziŵiri, musandimane zimenezo ndisanafe: Musalole kuti ndikhale wabodza kapena wonama. Ndisakhale mmphaŵi kapena khumutcha. Muzindidyetsa chakudya chondiyenera, kuwopa kuti ndikakhuta kwambiri, ndingayambe kukukanani nkumanena kuti, “Chauta ndiye yaninso?” Kuwopanso kuti ndikakhala mmphaŵi, ndingayambe kuba, potero nkuipitsa dzina la Mulungu wanga. Wantchito usamsinjirire kwa mbuyake, kuti angakutemberere, ndipo iweyo ungapezeke kuti ndiwe wolakwa. Pali ena amene amatemberera atate ao, ndipo sadalitsa amai ao. Pali ena amene amadziyesa oyera mtima, koma sadachotse zoipa zao. Pali ena amene amadzitukumula kwambiri, amadziyesa abwino kwabasi. Pali ena amene amasongola mano ao ngati malupanga, amaŵanola ngati mipeni, kuti adye amphaŵi ndi kuŵachotsa pa dziko lapansi, kutinso achotse anthu osauka pakati pa anzao. Mtsundu uli ndi ana aakazi aŵiri. Anawo amangokhalira kulira kuti, “Tipatseni chakuti, tipatseni chakuti.” Pali zinthu zitatu zimene sizikhuta. Pali zinthu zinai zimene siziti, “Takwana.” Manda, mkazi wosabala, nthaka yachiwumire ndiponso moto womangoyakirayakira. Aliyense amene amaseka bambo ndi kumanyozera kumvera mai, makwangwala akuchigwa adzamkoloola maso, ndipo mphungu zidzadya mnofu wake. Pali zinthu zitatu zimene zimandidabwitsa kwambiri. Pali zinthu zinai zimene sindizimvetsa konse, zinthuzo ndi izi: M'mene umaulukira mphamba mu mlengalenga, m'mene imayendera njoka pa thanthwe, m'mene chimayendera chombo pa nyanja yakuya, ndiponso m'mene mwamuna amachitira akakhala ndi namwali. M'mene amachitira mkazi akachita chigololo amatere: amati akadya nkupukuta pakamwa, namanena kuti, “Palibe chimene ndalakwa.” Pali zinthu zitatu zimene dziko lapansi limanjenjemera nazo. Pali zinthu zinai zimene dziko lapansi silingathe kuzipirira: kapolo akasanduka mfumu, chitsiru chikakhuta, mkazi wonyozeka akakwatiwa, ndiponso mdzakazi akalanda malo a mbuyake. Pali zinthu zinai zing'onozing'ono pa dziko lapansi, koma ndi zochenjera kwambiri: Nyerere zili ngati anthu opanda nyonga, komabe zimakonzeratu chakudya chake m'chilimwe. Mbira zili ngati anthu opanda nyonga, komabe zimakonza pokhala pake m'matanthwe. Dzombe lilibe mfumu, komabe lonse limakhala m'magulumagulu poyenda. Buluzi ungathe kumugwira ndi manja, komabe amakhala m'nyumba za mafumu. Pali zinthu zitatu zimene zimayenda chinyachinya. Pali zinthu zinai zimene zimayenda monyadira: Mkango umene uli ndi mphamvu kupambana nyama zonse, ndipo suthaŵa kanthu kalikonse. Tambala woyenda chinyachinya, ndi tonde, ndiponso mfumu yoyenda pakati pa anthu ake. Ngati wakhala ukupusa ndi kumadzikweza, kapena wakhala ukukonzekera kuchita zoipa, yamba wati chete, uziganize bwino. Paja ukakuntha mkaka, mafuta amapangika. Ukapsinya mphuno, magazi amatuluka, ndipo ukautsa mkwiyo, mikangano imaoneka. Naŵa mau a mfumu Lemuwele wa ku Masa amene adamphunzitsa mai wake: Nchiyani, mwana wanga? Nchiyani, mwana wa m'mimba mwanga? Nchiyani, mwana wanga amene ndidachita kukupempha polonjeza ndi malumbiro? Mphamvu zako usathere pa akazi, usamayenda nawo ameneŵa, amaononga ndi mafumu omwe. Iwe Lemuwele, mafumu sayenera kumamwa vinyo, olamulira asamalakalaka zakumwa zaukali, kuwopa kuti angaiŵale malamulo a dziko, ndi kukhotetsa zinthu zoyenerera anthu osauka. Munthu amene ali pafupi kufa, uzimpatsa chakumwa chaukali, ndipo munthu amene ali pa mavuto oopsa, uzimpatsa vinyo. Amwe kuti aiŵale umphaŵi wake asakumbukirenso kuvutika kwake. Munthu wosalankhula umlankhulire ndiwe. Anthu osiyidwa uŵalankhulire pa zoŵayenerera. Uzilankhula ndi kuweruza mwachilungamo. Uziteteza amphaŵi ndi osauka. Kodi mkazi wolemerera angathe kumpeza ndani? Ndi wokwera mtengo kuposa miyala ya yamtengowapatali. Mtima wa mwamuna wake umamkhulupirira, ndipo mwamunayo sadzasoŵa phindu. Masiku onse a moyo wake, mkaziyo amachitira mwamuna wake zabwino osati zoipa. Amanka nafunafuna ubweya ndi thonje, ndipo amagwira ntchito ndi manja ake mwaufulu. Ali ngati zombo za anthu amalonda, zakudya zake amakazitenga kutali. Amadzuka usikusiku nkuyamba kukonzera chakudya anthu a pabanja pake, ndi kuŵagaŵira ntchito adzakazi ake. Amalingalira za munda, naugula. Amalima munda wamphesa ndi ndalama zozipeza ndi manja ake. Amavala dzilimbe ndipo sachita manja khoba pogwira ntchito. Amazindikira kuti malonda ake ndi aphindu, choncho nyale yake sizima usiku wonse. Thonje amadzilukira yekha, ndipo nsalu amadziwombera yekha. Anthu osauka amaŵachitira chifundo, amphaŵi amaŵapatsa chithandizo. A pabanja pake saŵaopera kuti nkufa nacho chisanu, poti amadziŵa kuti onsewo amavala zovala zofunda. Amadzipangira yekha zofunda, ndipo iye amavala zovala zabafuta ndi za mtengo wapatali. Mwamuna wake ndi wodziŵika ndithu ku mabwalo, akakhala pakati pa akuluakulu a dziko. Mkazi ameneyu amasoka zovala za nsalu yabafuta, nazigulitsa, amaperekanso mipango kwa anthu amalonda. Mphamvu ndi ulemu zimakhala ngati chovala chake. Amaganiza zakutsogolo mosangalala. Amalankhula mwanzeru, ndipo amaphunzitsa anthu ndi mau okoma. Amayang'anira makhalidwe a anthu a pabanja pake, ndipo sachita ulesi mpang'ono pomwe. Ana ake amamnyadira nkumutchula kuti ndi wodala. Mwamuna wake nayenso amamtamanda, amati, “Inde alipo akazi ambiri olemerera kwabasi, koma kuyerekeza ndi iwe, onsewo nchabe.” Nkhope yachikoka ndi yonyenga, kukongola nkosakhalitsa, koma mkazi woopa Chauta ndiye woyenera kumtamanda. Muzimlemekeza chifukwa cha zochita zake, ntchito zake zizimpatsa ulemu ku mabwalo. Naŵa mau a Mlaliki, mwana wa Davide, mfumu ya ku Yerusalemu: Zonse nzopanda phindu, akutero Mlaliki. Zonse nzachabechabe! Ndithudi zonse nzopandapake. Kodi munthu amapindulanji ndi ntchito zonse zolemetsa zimene amazigwira pansi pano? Mbadwo wina ukutha, wina ukudza, koma dziko lapansi limakhalapobe losasinthika. Dzuŵa limatuluka, nkukaloŵa, ndipo limapita mwamsanga kumene linatulukira. Mphepo imaombera chakumwera, nkudzakhotera chakumpoto. Imaomba mozungulirazungulira, pozungulirapo nkudzabwereranso komwe yachokera. Mitsinje yonse imakathira ku nyanja, koma nyanjayo osadzaza. Kumene madzi adachokera amabwereranso komweko. Zinthu zonse nzolemetsa, kulemera kwake nkosasimbika. Maso sakhuta nkupenya, makutunso sakhuta nkumva. Zomwe zidaalipo kale ndizo zidzakhaleponso. Zomwe zidaachitika kale ndizo zidzachitikenso. Ndiye kuti chatsopano palibiretu pansi pano. Kodi chilipo chinthu chimene wina anganene kuti, “Ichi ndiye nchatsopano?” Iyai, chidaalipo kale, ifenso kukadalibe nkomwe. Zakale sizikumbukika, ngakhale zinthu zimene zidzachitike pambuyo pake sizidzakumbukikanso ndi amene adzabwere m'tsogolo mwake. Ine Mlalikine ndidakhalapo mfumu yolamulira Israele ku Yerusalemu. Ndidaaika mtima wanga pa kufunitsitsa kumvetsa bwino zonse zochitika pansi pano. Imeneyi ndi ntchito yolemetsa kwambiri imene Mulungu adatipatsa anthufe. Zonse zochitika pansi pano ndaziwona. Zonsezo nzopandapake, ndipo kuzifunafuna nkungodzivuta chabe. Chimene chidakhota sichingathe kuwongokanso, chimene palibe sichingathe kuŵerengedwa. Mumtima mwangamu ndinkati, “Ndatola nzeru zambiri, kupambana onse amene ankalamulira ku Yerusalemu kale. Ndaphunzira zambiri zaluntha ndi zanzeru.” Ndidaayesetsa kumvetsa kuti nzeru nchiyani, misala nchiyani, uchitsiru nchiyani. Koma ndidazindikira kuti kuterokonso kunali kungodzivuta chabe. Paja nzeru zambiri zimadzetsa chisoni chambiri, munthu akamaonjezera nzeru, ndiye kuti akuwonjezeranso chisoni. Nthaŵi zina mumtima mwangamu ndinkati, “Ah! Tsopano ndiyesepo zokondweretsa, ndidzisangalatse.” Koma ai, zimenezinso zinali zopanda phindu. Kukakhala kuseka, ndidati, “Imene ija ndi misala.” Chikakhala chisangalatso, ndidati, “Phindu lake nchiyani?” Potsata nzeruzo ndidaayesa kudzisangalatsa ndi vinyo, koma umenewo unali uchitsiru. Ndinkati mwina kapena njira yotere nkukhala yopambana, imene anthu amatsata pofuna kusangalala pa masiku oŵerengeka a moyo wao. Ndidaachita ntchito zazikulu. Ndidaamanga nyumba zambiri, ndi kudziwokera mipesa. Ndidaalima madimba ndi minda ya mitengo. Ndidaabzalamo mitengo yazipatso ya mitundu yonse. Ndidaakumbanso maiŵe oti madzi ake azithirira minda ya mitengo yobzala ija. Ndidaagula akapolo ndi adzakazi, ndinalinso ndi akapolo obadwira m'nyumba mwanga momwe. Ndinali ndi ng'ombe ndi nkhosa kupambana aliyense amene adalamulirapo ku Yerusalemu kale. Ndidaadzikundikiranso siliva ndi golide ndiponso chuma chochokera kwa mafumu amene ndinkaŵalamulira. Ndinali ndi ondiimbira nyimbo, amuna ndi akazi omwe. Ndinalinso ndi akazi aang'ono ochuluka, aja amasangalatsa mitima ya amunaŵa. Ndidaasanduka munthu wotchuka, nkudzapambana onse amene ankalamulira ku Yerusalemu kale, monsemo nzeru osandichoka. Chilichonse chimene maso anga ankachilakalaka, ndidaachitenga. Mtima wanga sindidaumane zokondweretsazo, pakuti mtima wangawo unkakondwa ndi ntchito zanga zonse zolemetsa. Zimenezi zinali mphotho ya ntchito zanga zolemetsazo. Tsono ndidayamba kulingalira zonse zimene ndidazichita, ntchito zolemetsa zonse zimene ndidazigwira, nkuwona kuti zonsezo zinali zopanda phindu. Kunali kungodzivuta chabe. Ndithu panalibe choti nkupindulapo pa dziko lapansi. Pamenepo ndidayesanso kulingalira kuti kwenikweni nzeru nchiyani, misala nchiyani, uchitsiru nchiyani. Kodi munthu wodzaloŵa ufumu tsopanoyo angapose bwanji mnzake adapita uja? Nzokhazokhazo zomwe ameneyo adazichita kale. Ndidaona kuti inde nzeru nzopambana uchitsiru, monga momwe kuŵala kumapambanira mdima. Inde munthu wanzeru amayenda maso ali patsogolo, pamene chitsiru chimayenda m'chimbulimbuli. Komabe ndidazindikira kuti zomwe zagwera winayo, mnzakeyonso zimamgwera zomwezo. Ndiye ine ndidayamba kulingalira kuti, “Kani zimene zimagwera chitsiru nanenso zidzandigwera zomwezo! Nanga tsono ineyo nzeru zambiri chotere nzanji?” Pamenepo ndidaona kuti zimenezinso nzopanda phindu! Pakuti munthu wanzeru, pamodzi ndi chitsiru chomwe, onsewo sakumbukika nthaŵi yaitali, pokhala kuti pa masiku akutsogolo, onsewo adzaiŵalika. M'mene chimafera chitsiru ndi m'menenso amafera munthu wanzeru. Motero moyo wanga ndidaipidwa nawo, chifukwa chakuti zonse zochitika pansi pano zimandimvetsa chisoni. Ndithudi, zonsezo nzopandapake, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungodzivuta chabe. Ntchito zanga zonse zolemetsa zimene ndidazigwira pansi pano zidandiipira, chifukwa ndiyenera kuzisiyira amene adzabwere pambuyo panga. Tsono ndani amadziŵa kuti munthu ameneyo adzakhala wanzeru kapena chitsiru? Komabe munthuyo adzakhala womalamulira zonse zimene ndidazichita pansi pano mwa nzeru zanga. Zimenezinso nzopanda phindu. Motero ndidayamba kutaya mtima chifukwa cha ntchito zonse zimene ndidazigwira movutikira pansi pano. Paja nthaŵi zina munthu amene wagwira ntchito zolemetsa mwaluntha, mwanzeru ndi mwaluso, zonsezo ayenera kuzisiyira munthu amene sadakhetserepo konse thukuta, kuti akondwere nazo. Zimenezinso nzopanda phindu, ndipo nzoipa kwambiri. Kodi munthu amapindulanji pa ntchito zonse zolemetsa ndi zodetsa nkhaŵa zimene amazichita pansi pano? Masiku ake onse amakhala achisoni, ntchito yake imakhala yovuta. Ndi usiku womwe mtima wake supumula. Zimenezinso nzopanda phindu. Kwa munthu palibe chabwino china choposa kudya, kumwa ndi kukondwerera ntchito zake. Ngakhale zimenezi ndazindikira kuti nzochokera kwa Mulungu. Nanga popanda Iye ndani angathe kudya, ndani angathe kusangalala? Pajatu munthu wokondweretsa Mulungu, Mulunguyo amamsandutsa waluntha, wanzeru ndi wosangalala. Koma wochimwa amampatsa ntchito yokunkha ndi younjika zinthu, kenaka zonsezo nkuzipatsa munthu wokondwetsa Mulungu. Zimenezinso nzopanda phindu, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungodzivuta chabe. Pansi pano chinthu chilichonse chili ndi nyengo yake ndi nthaŵi yake yomwe adaika Mulungu: pali nthaŵi yobadwa ndi nthaŵi yomwalira, pali nthaŵi yobzala ndi nthaŵi yozula zobzalazo. Pali nthaŵi yakupha ndi nthaŵi yochiritsa, nthaŵi yogwetsa ndi nthaŵi yomanga. Pali nthaŵi yomva chisoni ndi nthaŵi yosangalala, nthaŵi yolira maliro ndi nthaŵi yovina. Pali nthaŵi yokhala malo amodzi ndi nthaŵi yotalikirana, nthaŵi yokumbatirana ndi nthaŵi yoleka zokumbatiranazo. Pali nthaŵi yofunafuna ndi nthaŵi yotaya, nthaŵi yosunga ndi nthaŵi yomwaza. Pali nthaŵi yong'amba ndi nthaŵi yosoka, nthaŵi yokhala chete ndi nthaŵi yolankhula. Pali nthaŵi yokondana ndi nthaŵi yodana, nthaŵi ya nkhondo ndi nthaŵi ya mtendere. Kodi wantchito amapeza phindu lanji pa ntchito yake yolemetsa? Ndaziwona ntchito zimene Mulungu adapatsa anthu kuti azizigwira. Adapanga chinthu chilichonse kuti chikhale chabwino pa nthaŵi yake. M'mitima mwa anthu Mulungu adaikanso nzeru zotanthauzira zochitika za pa mibadwo ndi mibadwo. Komabe anthuwo sangathe kuzitulukira ntchito zonse za Mulungu kuyambira pa chiyambi mpaka pomalizira. Ndikudziŵa kuti kwa anthu palibe chabwino china choposa kukhala osangalala ndi kumadzikondweretsa nthaŵi yonse ya moyo wao. Ndi mphatso ya Mulungu kwa anthu kuti azidya, azimwa ndi kumakondwera ntchito zao zolemetsa. Ndikudziŵa kuti zimene Mulungu amazichita zimakhazikika mpaka muyaya. Palibe zimene zingathe kuwonjezedwa kapena kuchotsedwapo pa zimenezo. Mulungu adazipanga motero, kuti choncho anthu azimumvera. Zimene zilipo tsopano zidaaliponso kale. Zimene zidzakhalepo kutsogolo, zidaaliponso kale. Mulungu amabwezanso zakale zimene zidapita kuti zichitikenso. China chimene ndidachiwona pansi pano ndi ichi: Koyenera kukhala chiweruzo chabwino, komwekonso kumapezeka kuipa mtima. Koyenera kukhala chilungamo, komwekonso kumapezeka zoipa. Ndiye ine ndidayamba kulingalira kuti, “Mulungu adzaŵaweruza onse, abwino ndi oipa omwe, pakuti adaika nthaŵi yochitikira chinthu chilichonse ndiponso ntchito iliyonse.” Kunena za anthu, ndinkalingaliranso kuti, “Mulungu amaŵayesa ndi cholinga choti aŵaonetse kuti iwowo sasiyana konse ndi nyama. Zimene zimachitikira anthu, zomwezonso zimachitikira nyama. Monga chinacho chimafa, chinacho chimafanso. Zonsezo zimapuma mpweya umodzimodzi, munthu saposa nyama. Zonsezi nzopandapake. Zonse zimapita kumodzimodzi. Zonsezo nzochokera ku dothi, ndipo zimabwerera kudothi komweko. Kodi ndani angatsimikize kuti mzimu wa munthu ndiwo umakwera kumwamba, koma mpweya wa nyama umatsikira kunsi kwa nthaka? Choncho ndidaona kuti palibe chinthu chabwino kuposa kuti munthu azikondwerera ntchito yake, pakuti chake chenicheni nchimenechi. Ndani angathe kudziŵa chimene chidzamchitikire iye atafa?” Ndidaonanso kuzunza kulikonse kochitika pansi pano. Ndipo ndidaona ozunzidwa akulira misozi, koma panalibe ndi mmodzi yemwe woti aŵatonthoze. Panalibe oŵatonthoza chifukwa ozunzawo anali ndi mphamvu. Ndinkaganiza kuti akufa aja amene adapita kale ndi amwai kwambiri kupambana amene akadali ndi moyo. Koma wopambana onsewo ndi amene sadabadwe nkomwe, ndipo ntchito zoipa zimene zimachitika pansi pano sadaziwone. Tsono ndidazindikira kuti ntchito zonse zolemetsa ndiponso ntchito zonse zaluso zimachitika chifukwa choti wina akuchitira nsanje mnzake. Zimenezinso nzopanda phindu, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungodzivuta chabe. Paja akuti chitsiru chimangoti manja khodobala, nkumasoŵa chakudya mpaka kumafa ndi njala. Komabe nkwabwino kukhala ndi moyo wabata wodzaza dzanja limodzi, kupambana kutekeseka ndi ntchito zolemetsa zodzaza manja aŵiri, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungozivuta chabe. Ndidazindikira chinanso chopanda phindu pansi pano: Panali munthu amene anali yekha, wopanda mwana kapena mbale, komabe ntchito yake yolemetsa sinkatha. Maso ake sankakhutitsidwa nacho chuma chake. Motero sankadzifunsa konse kuti, “Kodi ntchito yolemetsa ndikuigwirayi ndiponso mavuto a kudzimana zokondweretsaŵa, ndikuchitira yani?” Zimenezi nzopanda phindu ndiponso nzosakondweretsa. Kukhala aŵiri nkwabwino koposa kukhala wekha, chifukwa ntchito ya anthu aŵiri ili ndi phindu lopambana. Aŵiriwo akagwa, wina adzautsa mnzake. Koma tsoka amene ali yekha: akagwa, ndiye kuti zavuta, chifukwa palibe wina womuutsa. Ndiponso aŵiri akagona pamodzi amafunditsana. Koma nanga mmodzi angathe kudzifunditsa bwanji? Nkotheka kuti munthu apambane mnzake amene ali yekha, koma pakakhala aŵiri, iwoŵa adzalimbana naye. Chingwe cha nkhosi zitatu sichidukirapo. Mnyamata wosauka ndi wanzeru ali bwino kupambana mfumu yokalamba ndi yopusa, imene siikumvanso malangizo. Mnyamatayo atha kukhala kuti adachita kuchokera ku ndende kudzaloŵa ufumu, kapenanso kuti adabadwa mmphaŵi m'dziko mwake momwemo. Ndinkaganiza za anthu onse amene amakhala pansi pano, ndipo ndidazindikira kuti pakati paopo panali mnyamata uja amene anali wodzatenga malo a mfumu. Mfumu ikhoza kulamulira anthu osaŵerengeka, komabe itamwalira, palibe aliyense amene adzayamikire zomwe mfumuyo idachita. Ndithudi, zimenezinso nzopandapake, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungodzivuta chabe. Uzisamala mayendedwe ako ukamapita ku Nyumba ya Mulungu. Kuli bwino kupita kumeneko kukaphunzirako, kupambana kukangopereka nsembe chabe ngati anthu opusa, amene sadziŵa kuti akuchita zoipa. Usamafulumira kulankhula, ndipo usamalumbira msanga kwa Mulungu mumtima mwako. Paja Mulungu ali Kumwamba, iwe uli pansi pano, tsono usamachulukitsa mau ai. Kuchuluka kwa mavuto mu mtima kumabweretsa maloto oipa, ndipo kuchuluka kwa mau kumadzetsa uchitsiru. Ukalumbira chinthu kwa Mulungu, usachedwe kuchichita, chifukwa Mulungu sakondwera nazo zitsiru. Zimene wazilumbira, uzichitedi. Kuli bwino kusalumbira kanthu kwa Mulungu, kupambana kuti ulumbire koma osachita. Pakamwa pako pasakuchimwitse, kuti choncho usayenerenso kukauza wansembe wa Mulungu kuti, “Ai, ndinkangonena!” Chifukwa chiyani ufuna kuputa Mulungu? Kodi ukufuna kuti aononge zimene wazigwirira ntchito? Maloto akachuluka pamachulukanso zokamba zachabechabe. Koma iwe uzilemekeza Mulungu. Ukamaona anthu osauka akuzunzika m'dziko, ndiponso anthu ena akupsinja anzao ndi kuŵalanda ufulu wao mwankhanza, usadabwe nazo zimenezo. Paja woyang'anira wokulapo ali naye wina wamkulu kwambiri amene amamuyang'anira. Ndipo palinso akuluakulu enanso oyang'anira iwowo. Alimi onse amatengako dzinthu dzam'minda, koma ndi mfumu yokha imene imaona phindu lake la mindayo. Anthu okonda ndalama sakhutitsidwa nazo ndalamazo. Chimodzimodzinso anthu okonda chuma, sakhutitsidwa nalo phindu. Zimenezinso nzachabechabe. Chuma chikachuluka, odya nawo chumacho amachulukanso. Nanga mwini wake amapindulapo chiyani? Si kumangoziyang'ana basi? Wantchito amagona tulo tabwino, ngakhale adye pang'ono kapena kudya kwambiri. Koma wolemera, chuma sichimgonetsa tulo. Pansi pano pali choipa china chomvetsa chisoni kwambiri chimene ndachiwona: Chuma chopweteka mwiniwake yemwe. Ndiye chuma chimenecho chikamwazika moipa, munthuyo nkukhala ndi ana, amachita kusoŵa choŵapatsa ana akewo. Monga momwe munthu adabadwira m'mimba mwa mai wake opanda kanthu, chonchonso adzapita maliseche. Pa zonse zimene adakhetsera thukuta, palibe nchimodzi chomwe chimene adzatenge m'manja mwake. Chimenechinso nchoipa chomvetsa chisoni kwambiri: kuti munthu adzapita monga momwe adabwerera. Nanga phindu lake nchiyani, popeza kuti iyeyo adagwira pachabe ntchito yolemetsa? Masiku ake onse moyo wake unali wodzaza ndi mdima ndi chisoni, unali moyo wa mavuto, matenda ndi nkhaŵa. Tsono chimene ndimachiwona kuti nchabwino ndi choyenera ndi ichi: kumadya, kumamwa, ndi kumakondwerera ntchito zonse zolemetsa zimene munthu umagwira pansi pano, pa masiku oŵerengeka a moyo wako amene Mulungu wakupatsa. Nchokhachi chimene ungati nchako, choyenera kulandira. Mwina Mulungu amamlemeretsa munthu pakumpatsa chuma ndi zabwino zina, namlola kuti akondwerere zonsezo. Munthuyo azilandire zimenezo ndi kumakondwerera ntchito zake zonse zolemetsa. Imeneyi ndi mphatso yochokeradi kwa Mulungu. Munthu wotereyu sadzaganizako kwenikweni za kuchepa kwa masiku a moyo wake, chifukwa chakuti Mulungu wamdzaza ndi chimwemwe mu mtima. Choipa china chimene ndachiwona pansi pano, chimene chimaŵaŵa anthu zedi, ndi ichi: Mulungu kukulemeretsa, kukupatsa chuma ndi ulemu, osasoŵa kanthu kalikonse kamene ukukalakalaka, koma tsono osakupatsa mwai woti udyerere zinthuzo, wodyerera nkukhala munthu wachilendo. Zimenezi nzothetsa nzeru, ndipo ndi vuto lokhumudwitsa kwambiri. Munthu ngakhale abale ana zana limodzi, nkukhala ndi moyo zaka zambiri, ngakhale zaka zakezo zichuluke chotani, ngati sakondwerera zinthu zabwino za pa moyo wake, potsiriza osalandira maliro aulemu, ndithu ine ndikuti munthuyo ngakhale mtayo womwe umpambana kwambiri. Mtayo umangopita pachabe nkuloŵa mu mdima, ndipo umakaiŵalika mumdimamo. Ngakhale mtayowo sudaone dzuŵa kapena kudziŵa kanthu kalikonse, komabe umapumula kupambana munthu wa moyo wautali uja, ngakhale akadakhala ndi moyo zaka zikwi ziŵiri, koma osaona zabwino. Kodi nanga onsewo suja amapita ku malo amodzimodzi? Munthu amagwira ntchito zolemetsa kuti apeze chakudya, komabe satha kukhutira kotheratu. Nanga munthu wanzeru ali ndi chiyani chimene amapambana nacho chitsiru? Kodi mmphaŵi amene amangodziŵa kukhala bwino pamaso pa anzake, ndiye kuti wapindulapo chiyani? Kuli bwino kumangopenya zinthu ndi maso kupambana kumazilakalaka chamumtima. Zimenezinso nzopanda phindu, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungodzivuta chabe. Chilichonse chimene chilipo adachitchula kale dzina. Za m'mene munthu aliri nzodziŵika, nchomveka kuti sangathe kutsutsana ndi amene ali wamphamvu kupambana iyeyo. Mau akachuluka, zopandapake zimachulukanso. Nanga munthu apindulapo chiyani? Ndani amadziŵa zomkomera munthu kwenikweni pa nthaŵi yochepa imene munthuyo ali ndi moyo? Moyo wake ndi wa masiku ochepa, ndi wopandapake, umangopitirira ngati mthunzi. Ndani angathe kumufotokozera munthuyo zimene zidzachitike pansi pano iyeyo atafa? Mbiri yabwino ndi yopambana mafuta onunkhira bwino amtengowapatali. Tsiku lomwalira ndi lopambana tsiku lobadwa. Kuli bwino kupita ku nyumba yamaliro kupambana kupita ku nyumba yamadyerero. Pakuti imfa ndiye mathero ake a anthu onse, tsono amoyo azisinkhasinkha bwino zimenezi. Chisoni nchabwino kupambana chimwemwe, chifukwa ngakhale nkhope ikhale yakugwa, mtima umathabe kutolapo nzeru. Mtima wa munthu wanzeru umalingalira kaŵirikaŵiri za imfa. Koma mtima wa munthu wopusa umalingalira za chimwemwe. Kuli bwino kuti munthu azimva kudzudzula kwa anthu anzeru, kupambana kumvera nyimbo zotamanda za zitsiru. Kuseka kwa zitsiru kuli ngati kuthetheka kwa moto kunsi kwa mbiya. Zimenezinso nzachabechabe. Ndithudi kuzunza ena kumamsandutsa munthu wanzeru kuti akhale wopusa, ndipo kulandira chiphuphu kumaononga mtima. Mathero ake a chinthu ndi abwino kupambana chiyambi chake. Mtima wopirira ndi wopambana mtima wodzikuza. Usamafulumira kukwiya, pakuti mkwiyo umakhalira zitsiru. Usamafunsa kuti, “Chifukwa chiyani masiku amakedzana anali abwino kupambana masiku ano?” Limeneli si funso lanzeru. Nzeru nzabwino ngati choloŵa chomwe, zimapindulitsa wamoyo aliyense pansi pano. Chitetezo cha nzeru chili ngati chitetezo cha ndalama. Koma kudziŵa zinthu kukuposerapo, chifukwa nzeru zimasunga moyo wa amene ali nazo. Taganizira ntchito ya Mulungu. Ndani angathe kuwongola chinthu chimene Iye adachipanga chokhota? Uzikondwa mwai ukakufikira, ndipo tsoka likakugwera uzilingalirapo bwino pamenepo. Udziŵe kuti ndi Mulungu yemwe amene amatumiza mwai ndi tsoka. Amatero kuti munthu asadziŵiretu zimene zidzachitike m'tsogolo. Pa moyo wanga wopandapakewu, ndaona zinthu ziŵiri izi: mwina anthu abwino amaonongeka, zabwino chichitirecho, mwinanso anthu oipa amakhala ndi moyo nthaŵi yaitali, zoipa chichitirecho. Ndiye usachite kunkitsa nako kulungama, kapena kunkitsa nazo nzeru. Nanga ufere ziti? Usachite kunyanyanso kuipa, usanyanye nawonso uchitsiru. Nanga uferenji nthaŵi yako isanakwane? Nkwabwino kuti utsate njira imodzi, komanso osataya njira inayo. Munthu woopa Mulungu adzapeza phindu ndi ziŵiri zonsezo. Nzeru zimapatsa munthu mphamvu zoposa zimene angampatse atsogoleri khumi amumzinda. Ndithudi, pa dziko lapansi palibe munthu amene amachita zabwino zokhazokha osachimwa konse. Usamasamala zonse zokamba anthu, mwinamwina udzamva wantchito wako akukutukwana. Mumtima mwako ukudziŵa kuti iweyonso udatukwanapo anthu ena. Zonsezi ndidaziyesa ndi nzeru zanga. Ndinkati, “Ndidzakhala wanzeru.” Koma nzeruzo zinali nane kutali. Zimene zilipo zili kutali ndipo nzozama, kuzamatu kwambiri. Ndani angathe kuzidziŵa? Motero ndidaikapo mtima kwambiri kuti ndidziŵe, ndifufuze ndi kumafunafuna nzeru ndi m'mene zinthu zimakhalira. Ndidafunanso kumvetsa kuipa kwake kwa uchitsiru ndiponso kupusa kwake kwa msala. Ndidapeza china choŵaŵa kupambana imfa. Chinthucho ndi mkazi amene ali ngati msampha, amene mtima wake uli ngati ukonde, ndipo manja ake ali ngati maunyolo. Munthu wokondweretsa Mulungu amamthaŵa mkaziyo, koma wochimwa amalolera kukhala kapolo wake. Zimenezitu nzimene ndidazipeza pakusonkhanitsa izi ndi izi, kuti ndidziŵe m'mene zinthu zimakhalira. Ndizo zimene mtima wanga unkazifunafuna kaŵirikaŵiri, koma osazipeza. Ndidapeza mwamuna mmodzi yekha wolungama pakati pa anthu 1,000, koma mkazi wolungama sindidampezepo ndi mmodzi yemwe pakati pa anthu onsewo. Ndidapeza chokhachi chakuti Mulungu pomulenga munthu, adampatsa mtima wolungama, koma anthu amatsata njira zaozao zambirimbiri. Ndani angafanefane ndi munthu wanzeru? Ndani angadziŵe kutanthauza zinthu? Munthu nzeru zake zimampatsa chimwemwe, ndipo ukali umachoka pankhope pake. Uzimvera lamulo la mfumu, ndipo chifukwa cha lumbiro lako kwa Mulungu usade nkhaŵa. Zinthu zikapanda kuikondweretsa mfumu, uchoke pamaso pake mwamsanga, pakuti imachita chilichonse chimene chikuikomera. Pajatu mau a mfumu ndi opambana. Ndani angafunse kuti, “Kodi mukuchita chiyani?” Womvera malamulo ake sadzaona vuto lililonse. Munthu wanzeru amadziŵa nthaŵi yake ndi njira yake yochitira zonse. Kanthu kalikonse kali ndi nthaŵi yake ndi kachitidwe kake, ngakhale kuti mavuto ake a munthu amamupsinja kwambiri. Palibe amene amadziŵa zimene zilikudza. Palibe amene angafotokozere zakutsogolo. Monga munthu alibe mphamvu zolamulira mpweya wa moyo, chonchonso alibe mphamvu zolamulira tsiku la kufa kwake. Nkhondo sithaŵika, tsono anthu ochita zoipa, kuipa kwaoko sikudzaŵapulumutsa. Zonsezi ndidaziwona pamene ndinkalingalira mumtima mwanga zonse zimene zimachitika pansi pano. Nthaŵi zonse pali ena amene amalamulira anzao mwankhanza. Pambuyo pake ndidaona oipa akuikidwa m'manda. Iwowo kale ankaloŵa ndi kumatuluka m'malo oyera, ndipo mumzindamo anthu ankaŵatamanda m'mene ankachita zinthu zoterezi. Zimenezinso nzachabechabe. Oweruza akamachedwetsa chilango cha anthu opalamula, anthu ena amalimba mtima nkumafuna kuti ayambe kuchita zoipa nawonso. Ngakhale kuti wochimwa amati akachita zoipa kambirimbiri, amakhalabe moyo nthaŵi yaitali, komabe ndikudziŵa kuti omvera Mulungu ndiwo amene zinthu zidzaŵayendere bwino, poti ndi amene amamlemekeza. Koma oipawo zinthu sizidzaŵayendera bwino, ndipo moyo wao udzakhala wosakhalitsa ngati mthunzi, poti samvera Mulungu. Pali chinthu china chachabechabe chimene chimachitika pansi pano. Chinthucho ndi ichi: mwina anthu abwino amalangidwa ngati ochita zoipa, pamene oipa amalandira zabwino ngati kuti ndi anthu abwino. Ndikuti zimenezinso nzachabechabe. Nchifukwa chake ndikuti munthu azikondwerera moyo, pakuti munthu alibe chinthu chinanso chabwino pansi pano choposa kudya, kumwa ndi kumadzikondweretsa. Akamatero, munthuyo adzakhala ndi chimwemwe pa ntchito yake masiku onse a moyo wake, amene Mulungu wampatsa pansi pano. Ndinkaikapo mtima kuti ndidziŵe nzeru ndi kumvetsa ntchito zimene zikuchitika pansi pano, osapeza tulo usana ndi usiku. Ndipo ndidaona ntchito zonse za Mulungu. Palibe munthu amene angathe kuzitulukira zonse zimene zimachitika pansi pano. Ngakhale munthu ayesetse chotani kuzimvetsa, sadzafikapo. Ngakhale munthu wanzeru anene kuti akudziŵa zinthu, nkosatheka kuti azitulukire. Zonse ndanenazi ndidazilingalirapo, ndipo ndidatsimikiza kuti anthu ochita chilungamo ndi anthu anzeru ali m'manja mwa Mulungu pamodzi ndi ntchito zao zomwe. Koma palibe munthu angadziŵe zimene zili m'tsogolo mwake, ngakhale zikhale za chikondi, kapena za chidani. Anthu onse zimene zidzaŵaonekere nzimodzimodzi, ochita chifuniro cha Mulungu ndi okana omwe, abwino ndi oipa, osamala zachipembedzo ndi osasamala omwe, opereka nsembe ndi osapereka omwe. Wabwino amafanafana ndi woipa. Wochita malumbiro amafanafana ndi woopa kulumbira. Chimene chili choipa kwambiri mwa zonse zochitika pansi pano ndi ichi chakuti tsoka limodzimodzi limagwera onse. Chinanso nchakuti mitima ya anthu njodzaza ndi zoipa. M'mitima mwao mumadzaza ndi zamisala pamene ali moyo, pambuyo pake kwao nkufa ndithu. Komabe amene ali ndi moyo ali nacho chikhulupiriro. Paja akuti ndiponi galu wamoyo kuposa mkango wakufa. Amoyo amadziŵa kuti adzafa, koma akufa sadziŵa kanthu, ndipo alibe mphotho inanso yoonjezera. Palibe ndi mmodzi yemwe woŵakumbukira. Chikondi chao, chidani chao ndi nsanje yao, zonse zidatha kale. Ndipo pa zonse zochitika pansi pano sadzalandirako kanthu konse mpakampaka. Ndiye iwe usaope, uzidya chakudya chako mokondwa, uzimwa vinyo wako ndi mtima wosangalala, pakuti Mulungu wavomereza kale zochita zakozo. Uzivala zovala zoyera nthaŵi zonse, uzidzola mafuta nthaŵi zonse. Uzikondwerera moyo pamodzi ndi mkazi amene umamkonda, pa masiku onse a moyo wako wopandapakewu umene Mulungu wakupatsa pansi pano. Ndi zokhazo zimene ungaziyembekeze pa moyo wako ndiponso pa ntchito zako zolemetsa zimene umazigwira pansi pano. Ntchito iliyonse imene ukuti uigwire, uigwire ndi mphamvu zako zonse. Pajatu kumanda kumene ukupitako kulibe ntchito, kulibe malingaliro, kulibe nzeru, ndiponso kulibe luntha. Ndidaonanso pansi pano kuti opambana pa kuthamanga si aliŵiro okhaokha, opambana pa nkhondo si amphamvu okhaokha, ndiponso okhala ndi chakudya si anzeru okhaokha. Olemera si odziŵa zambiri okhaokha, ndipo si anthu aluso okhaokha amene anzao amaŵakomera mtima. Onsewo mwai umangoŵagwera pa nthaŵi yake. Kungoti munthu saidziŵa nthaŵi yake. Monga momwe nsomba zimagwidwira mu ukonde, monga momwenso mbalame zimakodwera mu msampha, anthunso nchimodzimodzi. Amachita ngati kukodwa mu msampha pa nthaŵi yoipa, pamene tsoka laŵagwera mwadzidzidzi. Pansi pano ndidaonanso chinthu china chokhudza nzeru, ndipo ine ndidachiwona kuti nchinthu chachikulu. Panali mzinda waung'ono, m'mene munali anthu oŵerengeka. Tsono padafika mfumu yamphamvu kudzauthira nkhondo mzindawo, nkuuzinga ndi zithando zankhondo. Koma mumzindamo munali munthu wina wosauka koma wanzeru. Munthu ameneyo adaupulumutsa mzindawo ndi nzeru zakezo. Komabe panalibe ndi mmodzi yemwe amene adamkumbukira wosaukayo. Ndiye ine ndikuti nzeru nzabwino ndithu kupambana mphamvu, ngakhale kuti anthu sazimvera nzeru za munthu wosauka, ndipo za mau ake salabadako nkomwe. Mau a munthu wanzeru, olankhula mofatsa, ndi abwino kupambana kufuula kwa mfumu pa gulu la zitsiru. Nzeru nzabwino kupambana zida zankhondo, koma wochimwa mmodzi amatha kuwononga zabwino zambiri. Ntchentche zakufa zimaika fungo loipa m'mafuta onunkhira bwino. Choncho kupusa kwapang'ono kumatha kuwononga nzeru ndi ulemu. Mtima wa munthu wanzeru umamtsogolera bwino, koma mtima wa munthu wopusa umamsokeza. Chitsiru ngakhale chikamayenda mu mseu, zochita zake nzopanda nzeru ndithu, ndipo aliyense amachizindikira kuti nchitsirudi. Wolamula akakukwiyira, usachoke pa ntchito yako, pakuti kufatsa kumakonza ngakhale zolakwa zazikulu. Pansi pano pali choipa china chimene ndachiwona, choipa chake ndi cholakwa chimene amachichita wolamula. Opusa amaŵapatsa ntchito zapamwamba, olemera nkumaŵapatsa ntchito zotsika. Ndaona akapolo akuyenda pa akavalo, m'menemo akalonga akuyenda pansi ngati akapolo. Amene amakumba dzenje adzagwamo yekha. Amene amaboola khoma njoka idzamuluma. Amene amakumba miyala, itha kumpweteka miyalayo. Amene amaŵaza nkhuni, atha kudzipweteka nazo. Nkhwangwa ikakhala yobuntha, nkupandanso kuinola, imalira mphamvu zambiri potema. Koma nzeru zimathandiza munthu kuti athedi kudula kanthu. Nkopanda phindu kudziŵa kuseŵeretsa njoka ngati njokayo yakuluma kale. Mau a pakamwa pa munthu wanzeru amakondweretsa, koma pakamwa pa chitsiru mpoononga. Chitsiru chimayamba ndi mau opusa, potsiriza zolankhula zake zimangokhala zamisala basi. Chitsiru chimangochulutsa mau. Kodi ndani angadziŵe zimene zidzachitike kutsogolo? Ndani angathe kumuuza munthu zimene zidzachitike iye atafa? Chitsiru chimagwira ntchito modzitopetsa, koma njira yopita ku mzinda sichiidziŵa. Tsoka kwa iwe dziko, ngati mfumu yako ikali mwana, ndipo nduna zako zimachezera madyerero usiku wonse. Koma ndiwe wodala iwe dziko, ngati mfumu yako ndi mwana wa mfulu. Ndiwe wodala ngati nduna zako zimachita phwando pa nthaŵi yabwino, kuti zikhale zamphamvu, osati kuti ziledzere. Denga limaloshoka, mwini wake akakhala waulesi, ndipo nyumba imadontha, mwiniwake akakhala nthyamba. Phwando ndi lokondwetsa anthu, ndipo vinyo ndi wosangalatsa moyo. Komatu zonsezo nzolira ndalama. Ngakhale mumtima mwako usamainyoza mfumu. Ngakhale m'chipinda mwako momwe usamatukwana wolemera. Mwina kambalame kamumlengalenga kapena kachilombo kena kouluka nkukumvera, kenaka nkukaulula zonse kwa amene umaŵanenawo. Ndalama zako uziike pa malonda okagulitsa kutsidya kwa nyanja, ndipo udzapeza phindu patapita masiku ambiri. Ndalama zako uzisungize pa malo angapo, malo ambiri ndithu, pakuti sukudziŵa choipa chimene chidzaoneke pa dziko lapansi. Mitambo ikadzaza ndi madzi, kumagwa mvula. Mtengo ukagwera chakumwera kapena chakumpoto, kumene wagwerako kogonera nkomweko. Amene ayembekeza kuti mphepo ikhale bwino, kapena kuti mitambo ibwere bwino, sadzabzala ndipo sadzakolola kanthu. M'mene mzimu umaloŵera m'thupi la mwana m'mimba mwa mkazi wodwala, inu simudziŵa. Chonchonso ntchito ya Mulungu amene amapanga zonse, inu simungaidziŵe. M'maŵa uzifesa mbeu zako, ndipo madzulo usamangoti manja lende. Sudziŵa chimene chidzapindula, kaya ndi ichi kaya ndi chinachi, mwinanso ziŵiri zonsezo zitha kukhala zabwino. Kuŵala kwam'maŵa kumasangalatsa, ndipo maso ako akaona dzuŵa amakondwa. Munthu akakhala wa zaka zambiri, mlekeni akondwerere zaka zonsezo. Koma azikumbukira kuti masiku otsatira imfa yake ndi ochuluka koposa. Zonse zikudzazi nzopanda phindu. Anyamata inu, muzikondwerera unyamata wanu. Mitima yanu izisangalala pa nthaŵi ya unyamata wanu. Inde muzitsata zimene mtima wanu ukufuna, ndiponso zimene maso anu akupenya. Koma mudziŵe kuti pa zonsezo Mulungu adzakuweruzani. Choncho muchotseretu zokusautsani mu mtima mwanu, mupewe zokupwetekani m'thupi mwanu. Pajatu unyamata ndi ubwana, zonse nzopandapake. Uzikumbukanso Mlengi wako pa masiku a unyamata wako, masiku oipa asanafike, zisanafikenso zaka zoti uzidzati, “Moyowu wandikola.” Nthaŵi ya ukalamba wako, dzuŵa, kuŵala, mwezi, nyenyezi, zonse zidzakudera, ndipo mitambo idzabweranso mvula itagwa. Nthaŵi imeneyo miyendo yako izidzanjenjemera, manja ako adzafooka. Mano ako oŵerengekawo azidzalephera nkutafuna komwe, ndipo maso ako adzayamba kuchita chidima. Makutu ako adzatsekeka ndipo sudzamva phokoso lakunja. Sudzamvanso kusinja kwapamtondo kapena kulira kwa mbalame m'mamaŵa. Udzaopa kukwera pa malo apamwamba, ndipo nkuyenda komwe kudzakhala koopsa. Kumutu kudzangoti mbu, udzalephera nkuyenda kodziguza komwe, ndipo chilakolako chilichonse chidzakuthera. Tonse tikupita kwathu kokakhala mpaka muyaya, ndipo titapita kudzakhala kulira m'miseu yonse. Nthambo yasiliva idzamasuka, mbale yagolide idzasweka, mtsuko udzaphwanyika ku kasupe, ndipo mkombero udzathyoka ku chitsime. Pamenepo thupi lidzabwerera ku dothi monga m'mene lidaaliri, ndipo mzimu udzabwerera kwa Mulungu amene adaupereka. Nkuwonatu Mlaliki akuti, “Zonse nzopanda phindu. Ndithudi, zonse nzopandapake.” Chifukwa chakuti Mlalikiyo anali waluntha, adaphunzitsa anthu zambiri. Ankasinkhasinkha, kufufuzafufuza ndi kulongosola malangizo mosamala kwambiri. Mlalikiyo ankafunafuna mau ogwira mtima, ndipo adalemba mau oona ndi mtima wolungama. Mau a anthu anzeru ali ngati zisonga, ndipo zokamba zao zimene adasonkhanitsa zili ngati misomali yokhomerera kwambiri. Zolankhula zonsezo amapereka ndi Mbusa mmodzi yekha. Mwana wanga, uchenjere ndi kalikonse kobzola pamenepa. Kulemba mabuku sikutha, ndipo kuphunzira kwambiri kumatopetsa thupi. Basi, zonse zamveka. Mfundo yeniyeni ya zonsezi ndi iyi: Uzimvera Mulungu, ndipo uzitsata malamulo ake, pakuti umenewu ndiwo udindo wake wonse wa munthu. Pajatu Mulungu adzaweruza zonse zimene timachita, zabwino kapena zoipa, ngakhale ndi zam'chinsinsi zomwe. Nyimbo ya Solomoni, nyimbo yoposa nyimbo zonse. Mkazi Undimpsompsone ndi milomo yako, chifukwa chikondi chako nchoposa vinyo kukoma kwake. Mafuta ako odzola ngonunkhira bwino, dzina lako likundikumbutsa za mafuta otsanyukako. Nchifukwa chaketu, atsikana sangaleke kukukonda. Tenge, ndizikutsata, tiye tifulumire. Iwe mfumu yanga, kandiloŵetse m'chipinda mwako. Tizisangalala kwambiri ndi kukondwa limodzi. Chikondi chako tichitamande kupambana vinyo. Akazi onse amakukondera kaone! Inu akazi a ku Yerusalemu, ine ndine wakuda inde, komatu wokongola tsono. Ndine wakuda ngati mahema a ku Kedara, komabe wokongola ngati makatani a m'nyumba ya Solomoni. Musandiyang'ane monyoza chifukwa cha kudaku, ndi dzuŵatu lidandidetsali. Alongo anga adandikwiyira, mpaka kukandigwiritsa ntchito m'minda yamphesa. Koma munda wangawanga, osatha kuusamala. Tandiwuza, iwe wokondedwa wanga wapamtima, kumene umadyetsa ziŵeto zako, kumene umazigoneka masana. Nanga ndizingokhala ndili zunguliruzunguliru ku magulu a ziŵeto za abusa anzako! Mwamuna Iwe wokongola koposa akazi onsewe, ngati sukukudziŵa, uzingotsata m'makwalala a msambi wa ziŵeto, uzidyetsa mbuzi zako pambali pa mahema a abusawo. Iwe bwenzi langa, kukongola kwako, ngati akavalo a magaleta a Farao. Masaya ako akukongola ndi ndolo zam'makutuzi. Khosi lakonso likukongola ndi mikanda ya miyala yamtengowapatali. Tidzakupangira ukufu wagolide, wokhala ndi timakaka tasiliva. Mkazi Pamene mfumu inali gone podyera pake, mafuta anga onunkhira adapereka kafungo kachikoka. Wokondedwa wanga ndikumuwona ngati kathumba ka mure, kamene kamakhala pakati pa maŵere angaŵa. Wokondedwa wanga ndikumuwona ngati chipukutu cha maluŵa ofiira a m'munda wamphesa wa ku Engedi. Mwamuna Iwe bwenzi langa, ndiwe wokongola, ndiwe chiphadzuŵa. Maso ako akunga ngati nkhunda. Mkazi Wokondedwa wanga, nawenso ndiwe wokongola, wokongoladi zedi. Malo athu ogonapo ndi msipu wobiriŵira. Mitanda ya nyumba yathu ndi yamkungudza, phaso lake ndi la mtengo wa paini. Ndili ngati duŵa la ku Saroni, ngati kakombo wam'zigwa. Mwamuna Muja amakhalira kakombo pakati pa minga, ndi m'mene aliri wokondedwa wanga pakati pa atsikana. Mkazi Muja umakhalira mtengo wa apulosi pakati pa mitengo yam'nkhalango, ndi m'mene aliri wokondedwa wanga pakati pa anyamata. Ndinkakondwa kwambiri ndikausa mumthunzi mwake, zipatso zake zinali tseketseketseke m'kamwamu. Adanditenga kupita nane ku nyumba yaphwando, mbendera yake yozika pa ine inali chikondi. Mundidyetse mphesa zouma, munditsitsimutse ndi maapulosi, pakuti ndikumva chikondi chodwala nacho. Ha, ndidakakonda ineyo nditatsamira dzanja lake lamanzere, iyeyo nkundikumbatira ndi dzanja lamanja! Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndakupembani, pali mphoyo ndi nswala zakuthengo, chikondichi musachigwedeze kapena kuchiwutsa mpaka pamene chifunire ichocho. Mkazi Tamvani liwu la wokondedwa wanga! Taonani akubwera, akulumphalumpha pa mapiri, akujoŵajoŵa pa zitunda. Wokondedwa wanga ali ngati mphoyo, kapena mwanawambaŵala. Si uyo waimirira apoyo, kuseri kwa khoma lathulo, akusuzumira m'mawindo, akuyang'anira pa made a mawindo. Wokondedwa wanga akulankhula nkumandiwuza kuti: Mwamuna “Dzuka bwenzi langa, wokongola wanga, tiye tizipita. Ona, nyengo yachisanu yatha, mvula yatha ndipo yapitiratu. Maluŵa ayamba kuwoneka m'dziko, nthaŵi yoimba yafika, njiŵa zikumveka kulira m'dziko mwathu. Mikuyu ikubereka zipatso, mipesa ikuyamba maluŵa. Mitengoyo ikutulutsa fungo lokoma. Dzuka bwenzi langa, wokongola wanga, tiye tizipita. Iwe nkhunda yanga, yokhala m'ming'alu yam'matanthwe, yobisala m'phiri lotsetsereka, ntaonako nkhope yako, ntamvako liwu lako. Paja liwu lako nlomveka bwino, ndipo nkhope yako ndi yokongola. Mutigwirire nkhandwe, nkhandwe zing'onozing'ono, zimene zimatiwonongera minda yamphesa, pakuti mipesa yathu idachita maluŵa.” Mkazi Wokondedwa wangayo ndi wangadi, ndipo ine ndine wake. Amadyetsa gulu lake la ziŵeto pakati pa akakombo. Kamphepo kamadzulo kakamayamba kuuzira, mithunzi ikamayamba kuthaŵa, unyamuke, iwe wokondedwa wanga, uthamange ngati mphoyo, kapena ngati mwanawambaŵala pakati pa mapiri azigwembezigwembe. Usiku uliwonse ndili gone pabedi panga ndinkangomufunafuna amene mtima wanga umamkonda. Ndidamufunafuna koma osampeza. Ndidamuitana, koma iye osandiyankha. Ndiye ndidati, “Ai, tsopano ndidzuka ndi kuloŵa mu mzinda, m'miseu ndi m'mabwalo. Ndimufunafuna amene mtima wanga umamkonda.” Ndidamufunafunadi, koma osampeza. Alonda adandipeza pamene ankayendera mzinda. Ndidaŵafunsa kuti, “Kodi mwandiwonerako amene mtima wanga umamkonda?” Ndidangoti iwo aja ntaŵapitirira pang'ono, ndampeza amene mtima wanga umamkonda. Ndidamgwira, osamlola kuti achoke, mpaka nditamloŵetsa m'nyumba ya amai anga, m'chipinda cha amene adandibala. Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndakupembani, pali mphoyo ndi nswala zakuthengo, chikondichi musachigwedeze kapena kuchiwutsa mpaka pamene chifunire ichocho. Mkazi Kodi nchiyaninso icho chikutulukira ku chipululucho ngati utsi watolotolo, chonunkhira mure ndi lubani, chokhala ndi zonunkhira zonse zogulitsa anthu amalonda? Amenewo ndi machira a Solomoni. Pali ankhondo makumi asanu ndi limodzi, amuna anyonga a ku Israele operekeza. Onsewo agwira malupanga, ndipo ngodziŵa kumenya nkhondo, aliyense wavala lupanga pambali pake, kuti alimbane ndi aupandu usiku. Mfumu Solomoni adadzipangira machira a matabwa a ku Lebanoni. Milongoti yake adapanga yasiliva, kumbuyo kwake kunali kwagolide, pampando pake panali nsalu yofiirira. Tulukani, inu akazi a ku Ziyoni, mudzaone Mfumu Solomoni, atavala chisoti chaufumu chimene mai wake adamuveka pa tsiku la ukwati wake, tsiku limene mtima wake unkasangalala. Ndiwe wokongola, iwe wokondedwa wanga! Ndithuditu, ndiwe wokongoladi! Kumbuyo kwa nsalu yako yakumutuyo maso ako akuwoneka oŵala ngati nkhunda. Tsitsi lako likuchita pekupeku ngati mbuzi zoti zikutsetsereka pa mapiri a ku Giliyadi. Mano ako ali mbee ngati nkhosa zometa zoti angozisambitsa kumene. Mano onsewo ngoyang'anana bwino, palibe chigwelu nchimodzi chomwe. Milomo yako ili ngati mbota yofiira, ndipo pakamwa pako mpokongola zedi. Kukhalira kumbuyo kwa nsalu yako yakumutuyo, masaya ako, akuwoneka ngati mabandu a makangaza. Khosi lako lili ngati nsanja ya Davide, yomangidwa bwino ndipo yosalala. Mkanda wako wam'khosi, ngati zishango 1,000 zokoloŵeka kuzungulira nsanjayo. Maŵere ako ali ngati mbaŵala ziŵiri, ngati mphoyo zamapasa zimene zikudya pakati pa akakombo. Pamene kamphepo kamadzulo kakuyamba kuuzira, ndipo mithunzi ikuthaŵa, ndidzapita mofulumira ku phiri la mure, ndi ku chitunda cha lubani. Ndiwe wokongola kwabasi, iwe wokondedwa wanga. Ulibe nkachilema komwe. Tiye tichokeko ku Lebanoni, iwe mkazi wanga. Tiye tichoke ku Lebanoni kuno, utsagane ndi ine. Utsikepo pa nsonga ya phiri la Amana, pa nsonga ya phiri la Seniri ndi la Heremoni. Uchokemo m'mapanga a mikango, uchokeko ku ngaka za akambuku. Iwe mlongo wanga, iwe mkazi wanga, wangoti mtima wangawu kwe! Wanditenga mtima ndi kapenyedwe ka maso ako, ndiponso ndi mphande imodzi ya mkanda wa m'khosi mwako. Iwe mlongo wanga, iwe mkazi wanga, chikondi chako nchosangalatsa. Chikondi chako nchosangalatsa kupambana vinyo, mafuta ako ndi onunkhira bwino kupambana zonunkhira zabwino zonse. Iwe mkazi wanga, milomo yako ili uchi mvee! Kunsi kwa lilime lako kuli ngati uchi ndi mkaka. Fungo la zovala zako likumveka ngati fungo la ku Lebanoni. Iwe mlongo wanga, iwe mkazi wanga, uli ngati munda wopiringidza, ngati munda wopiringidza, ngati kasupe wochingidwa. Kumeneko mbeu zimakondwa bwino. Munda wake, ngati dimba la makangaza lokhalanso ndi zipatso zokoma zamitundumitundu, ndi maluŵa amitundumitundu. Kuli mitengo ndi zitsamba zosiyanasiyana zopangira zonunkhira zabwino kwambiri. Iwe uli ngati kasupe wothirira munda, ngati chitsime cha madzi abwino, ngati mitsinje yamadzi yochokera ku Lebanoni. Mkazi Dzuka, iwe mphepo yakumpoto, bwera kuno, iwe mphepo yakumwera. Uuzire pa munda wanga kuti fungo lake lokoma likwanire ponseponse. Wokondedwa wanga aloŵe m'munda mwake, adye zipatso zake zokoma. Ndaloŵa m'munda mwanga, iwe mlongo wanga, iwe mkazi wanga. Ndikukolola mure wanga ndi zokometsera chakudya. Ndikudya uchi wanga pamodzi ndi zisa zake zomwe. Ndikumwa vinyo wanga ndi mkaka wanga. Akazi Inu apaubwenzi, idyani ndi kumwa: Inu okondana, imwani kwambiri! Mkazi Kugona ndinagona, koma mtima wanga unali maso. Tamverani! Wokondedwa wanga akugogoda. Mwamuna “Tanditsekulira iwe mlongo wanga, iwe wokondedwa wanga, iwe nkhunda yanga, iwe wangwiro wanga. Mutu wanga wanyowa ndi mame, tsitsi langa lachita madzi chifukwa cha nkhungu yausiku.” Mkazi Zovala ndavula kale, ndingazivalenso bwanji? Ndasamba kale m'miyendo, nanga ndiidetsenso poyenda? Pamene wokondedwa wanga adangoti pisu dzanja pa chiboo chapachitseko, mtima wanga udachita kuti phwii! Ndidanyamuka kukamtsekulira wokondedwa wanga, manja anga ali noninoni ndi mure. Zalazi zili mure chuchuchu pa zogwirira za mpiringidzo. Ndidamtsekulira wokondedwa wanga, koma nkuti iyeyo atachokapo, atapita. Pamene iye ankalankhula, mtima wanga udangoti fumu! Ndidamfunafuna koma osampeza. Ndidamuitana, koma iye osandiyankha. Alonda adandipeza pamene ankayendera mzinda. Adandimenya mpaka kundipweteka. Alonda apamalingawo adandilanda mwinjiro wanga. Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndakupembani, mukampeza wokondedwa wangayo mumuuze kuti ine ndikumva chikondi chodwala nacho. Akazi Iwe wokongola koposa akazi onsewe, kodi wokondedwa wakoyo ngwopambana wina aliyense bwanji? Kodi wokondedwa wakoyo ngwopambana ena onse chotani kuti uzichita kupemba motere? Mkazi Wokondedwa wangayo ngwokongola, ndiponso wathanzi, wodziŵika zedi pakati pa amuna zikwi khumi. Mutu wake uli ngati golide wosalala kwambiri. Tsitsi lake nlopotana bwino, lakuda bwino ngati nthenga za khwangwala. Maso ake amaoneka okongola ngati nkhunda zitakhala pa akasupe a madzi, ngati nkhunda zitasamba mu mkaka, zitangoima bwinobwino. Masaya ake ali ngati timinda ta mbeu zokometsera chakudya, zopatsa fungo lokoma. Milomo yake ili ngati akakombo, ili noninoni ndi zodzoladzola za mure. Mikono yake ili ngati nthambi zagolide za makaka a miyala yamtengowapatali. Thupi lake nlosalala ngati mnyanga wanjovu woti aikamo miyala ya safiro. Miyendo yake ili ngati mizati yamwala yokhazikika pa maziko agolide. Ali ndi maonekedwe aulemerero ngati mapiri a ku Lebanoni, maonekedwe aulemu ngati mitengo ya paini ya pamapiripo. Milomo yake njosangalatsa kwambiri, munthuyo amanditenga mtima kwabasi. Ameneyutu ndiye wokondedwa wanga, ndiponso bwenzi langa, inu akazi a ku Yerusalemu. Iwe wokongola koposa akazi onsewe, kodi wokondedwa wakoyo wapita kuti? Kodi wokondedwa wakoyo waloŵera potani, kuti tichite kukuthandiza kumfunafuna? Mkazi Wokondedwa wanga watsikira kumunda kwakeku, ku timinda ta mbeu zokometsera chakudya. Akukadyetsa ziŵeto zake ku minda ndiponso akukathyola akakombo. Wokondedwa wangayo ine ndine wake, ndipo iyeyo ndi wangawanga. Amadyetsa ziŵeto zake pakati pa akakombo. Mwamuna Iwe bwenzi langa, ndiwe wokongola ngati Tiriza, wa maonekedwe abwino ngati Yerusalemu, ndiwe wochititsa mantha ngati gulu la ankhondo mbendera zili m'manja. Usandipenyetsetse, pakuti maso ako amanditenga mtima. Tsitsi lako likuchita pekupeku ngati mbuzi, zoti zikutsetsereka pa mapiri a ku Giliyadi. Mano ako ali mbee ngati nkhosa zometa, zoti angozisambitsa kumene. Mano onsewo ngoyang'anana bwino, palibe chigwelu nchimodzi chomwe. Kukhalira kumbuyo kwa nsalu yako yakumutuyo, masaya ako akuwoneka ngati mabandu a makangaza. Mfumu ili ndi akazi enieni makumi asanu ndi limodzi, ili ndi akazi aang'ono makumi asanu ndi atatu, ilinso ndi anamwali tayetaye! Koma ine nkhunda yanga, wangwiro wanga, ndi mmodzi yekha basi, mwana mmodzi yekha wa amai ake, mwana wapamtima wa amai ake. Anamwali atamuwona, adamutcha wodala. Akazi enieni a mfumu ndi akazi onse aang'ono adamtamanda. Ndani uyu wooneka ngati mbandakuchayu, wokongola ngati mwezi, woŵala ngati dzuŵa, wochititsa mantha ngati gulu la ankhondo mbendera zili m'manja? Ndidatsikira ku munda wa mitengo ya alimondi, kuti ndikayang'ane maluŵa akuchigwa, kuti ndikaone ngati mipesa idaphukira, ngati makangaza adachita maluŵa. Ndisanazindikireko kanthu, ndidakhala ngati ndikulota kuti ndili m'galeta pambali pa mfumu yanga. Akazi Bwerera, bwerera, iwe namwali wa ku Sulami, bwerera kuti tidzakupenyetsetse. Mkazi Chifukwa chiyani mukuti mudzandipenyetsetse ine Msulamine, pamene ndikuvina pakati pa magulu aŵiri? Iwe namwali wachifumu, mapazi ako ngokongola m'nsapato wavalazo. Ntchafu zako nzoulungika bwino ngati miyala yamtengowapatali, yosemedwa ndi mmisiri waluso. Mchombo wako uli ngati chikho choulungika, chimene nthaŵi zonse nchodzaza ndi vinyo wabwino. Pamimba pako mponing'a ngati mtolo wa tirigu wozingidwa ndi akakombo. Maŵere ako akuwoneka ngati mbaŵala ziŵiri, ngati mphoyo zamapasa. Khosi lako lili see ngati nsanja ya mnyanga wanjovu. Maso ako ali ngati maiŵe a ku Hesiboni, amene ali pafupi ndi chipata cha ku Batirabimu. Mphuno yako ikuwoneka ngati nsanja ya ku Lebanoni, yoyang'ana ku Damasiko. Mutu wako uli bwinobwino neng'a, ngati phiri la Karimele, ndipo tsitsi lako lalitali lili chezichezi. Kukongola kwake kumatha kudolola ndi mfumu yomwe. Ndiwe wokongola zedi, ndiponso wosangalatsa, iwe wokondedwawe, namwali wokondweretsawe. Msinkhu wako uli ngati mtengo wa mgwalangwa, maŵere ako ali ngati masango a zipatso zake. Ndidati, ndikwera mu mtengo wa mgwalangwawu, ndikathyole zipatso zake. Maŵere ako akhale ngati masango a mphesa, fungo la mpweya wako likhale lonunkhira bwino ngati la maapulosi. Ukamandimpsompsona, ine kukhosi see, ngati ndikumwa vinyo wokoma kwambiri. Mkazi Tsono vinyo ameneyu amthirire wokondedwa wanga, ayenderere pa milomo yake ndi m'mano mwake. Wokondedwayo ine ndine wake, chilakolako chake chonse chili pa ine. Bwera, wokondedwa wanga, tiye tiloŵe m'minda, tikagone ku midzi. Tiye tilaŵirire m'mamaŵa kupita ku minda yamphesa, tikaone ngati mipesa idaphuka, ngati nkhunje zake zidachita maluŵa, ndiponso ngati makangaza adachita maluŵa. Kumeneko ndidzakuwonetsa chikondi changa. Mitengo ya mankhwala a chisulo imapereka fungo labwino, pakhomo pathu pali zipatso zokoma zonse, zimene ndakusungira, iwe wokondedwa wanga. Ha! Achikhala unali mlongo wanga, woyamwa bere limodzi ndi ine! Ndikadakumana nawe panjira, bwenzi ntakumpsompsona, ndipo wina aliyense sakadandinyoza. Ndikadakutenga nkukuloŵetsa m'nyumba ya amai anga, m'chipinda cha amene adandibala. Ndikadakupatsa vinyo wotsekemera kuti umwe, ndi madzi a makangaza. Ine ndikadatsamira dzanja lako lamanzere, iwe nkundikumbatira ndi dzanja lamanja. Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndakupembani, chikondichi musachigwedeze kapena kuchiwutsa mpaka pamene chifunire ichocho. Akazi Kodi ndani uyo akutuluka ku chipululuyo, atatsamira wokondedwa wake? Mkazi Ndidakudzutsa patsinde pa mtengo wa apulosi uja. Pamenepo mpamene amai ako adachirira pokubala iweyo. Umatirire mtima wako kuti musaloŵe winanso koma ine ndekha, ndipo sudzakumbatira winanso koma ine ndekha. Paja chikondi nchamphamvu ngati imfa, nsanje njaliwuma ngati manda. Chikondi chimachita kuti laŵilaŵi ngati malaŵi a moto, ndipo nchotentha koopsa. Ngakhale madzi ochuluka sangachizimitse chikondi, ngakhale madzi a chigumula sangachikokolole. Ngakhale munthu atapereka chuma chonse cha m'nyumba chifukwa chofuna kugula chikondi, adzangonyozeka nazo kotheratu. Alongo a Mkazi Tili naye ife mlongo wathu wamng'ono, alibe ndi maŵere omwe. Tidzamchitira chiyani mlongo wathu pa tsiku limene adzamfunsire mbeta? Iye akakhala ngati khoma, tidzammangira nsanja yasiliva. Koma akakhala ngati chitseko, tidzamchinga ndi matabwa amkungudza. Mkazi Ine ndili ngati khoma, ndipo maŵere anga ali ngati nsanja zake. Tsono m'maso mwa wokondedwa wanga ndili ngati wodzetsa mtendere. Mwamuna Solomoni anali ndi munda wamphesa ku Baala-Hamoni. Mundawo adaubwereka alimi. Aliyense mwa iwo ankayenera kupereka ndalama zasiliva chikwi chimodzi kuti azilimamo. Koma munda wanga wamphesa ndi wangawanga, ndiponso wa ine ndekha. Iwe Solomoni, khala nazo ndalama chikwi chimodzi zija, khala nawonso alimi ako mazana aŵiri aja. Iwe amene umakhala m'munda anzanga akumvetsera kuti amve liwu lako. Tandilola kuti ndilimve. Mkazi Fulumiratu wokondedwa wanga, khala ngati mphoyo kapena ngati mwanawambaŵala wothamanga m'mapiri, m'mene mumamera mbeu zokometsera chakudya. Buku lino likufotokoza zinthu zimene Mulungu adaululira Yesaya, mwana wa Amozi, zokhudza Yuda ndi Yerusalemu pa masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a ku Yuda. Chauta adati, “Tamvera, iwe mlengalenga, tchera khutu, iwe dziko lapansi, Ine Chauta ndikulankhula. Ndidabereka ana ndi kuŵalera, koma andigalukira. Ng'ombe imadziŵa mwini wake, bulu amadziŵa kumene mwini wake amamdyetsera, koma Aisraele sadziŵa, anthu anga samvetsa konse.” Ha, mtundu wochimwa, inu anthu olemedwa ndi machimo, obadwa kwa anthu ochita zoipa, ana omira m'zoipa! Mudasiya Chauta, mudanyoza Woyera uja wa Israele, mudamufulatira kwathunthu. Kodi ndi pati ndingakumenyeninso, popeza kuti mukupandukirapandukira? Aliyense mutu wake uli ndi mabala kale, ndipo mtima wake wafookeratu. Kuchokera kuphazi mpaka kumutu palibe pabwino, ponse pali mikwingwirima ndi zilonda, mabala ali magazi chuchuchu. Mabala ake ngosatsuka, ngosamanga, ndiponso ngosapaka mafuta ofeŵetsa. Dziko lanu lasanduka bwinja, mizinda yanu aitentha. Alendo akukuwonongerani dziko inu muli pomwepo. Lasanduka bwinja, lagonjetsedwa ndi alendo. Mzinda wa Yerusalemu watsala wokhawokha ngati nsanja m'munda wamphesa, ngati dinda m'munda wa minkhaka, ngatinso mzinda wozingidwa ndi nkhondo. Chauta Wamphamvuzonse akadapanda kutipulumutsirako ena oŵerengeka, tikadaonongeka kotheratu ngati anthu a ku Sodomu ndi Gomora. Tsono imvani zimene Chauta akukuuzani, inu akulu a ku Sodomu. Mvetsetsani zimene Mulungu wathu akukuphunzitsani, inu anthu a ku Gomora. Chauta akuti, “Kodi ndili nazo chiyani nsembe zanu zochuluka? Zandikola nsembe zopsereza za nkhosa zamphongo ndi za mafuta a nyama zonenepa. Sindikuŵafunanso magazi a ng'ombe zamphongo ndi a anaankhosa ndi a atonde. “Ndani amakulamulani kuti mubwere nazo zimenezi pamaso panga? Ndani amakuuzani kuti muzipondaponda m'mabwalo a Nyumba yanga? Musabwere nazonso nsembe zanu zachabechabe. Utsi wake umandinyansa. Sindingapirire misonkhano yanu yamapemphero, kapenanso zikondwerero za pokhala mwezi ndi za Sabata, sindingapirire mapemphero oipitsidwa ndi machimo. Zikondwerero zanu za pokhala mwezi ndi masiku anu oyera ndimadana nazo. Zasanduka katundu wondilemera, ndatopa nako kuŵapirira. Mukamatambasula manja anu popemphera, sindidzayang'anako. Ngakhale muchulukitse mapemphero anu chotani, sindidzasamalako, chifukwa manja anu ndi odzaza ndi magazi. Sambani, dziyeretseni, chotsani pamaso panga ntchito zanu zoipa. Inde, lekani kuchita zoipa. Phunzirani kuchita zabwino. Funafunani chilungamo, opsinjidwa muŵathandize. Tetezani ana amasiye, muŵaimirire pa milandu yao akazi amasiye.” Chauta akunena kuti, “Tiyeni tsono tikambe mlandu wanu: chifukwa cha machimo anu mwafiira kwambiri, koma Ine ndidzakutsukani, inu nkukhala oyera kuti mbee. Mwachita kuti psuu ngati magazi, koma mudzakhala oyera ngati thonje. Ngati muli okonzeka kundimvera, mudzalidyera dziko. Koma mukakana ndi kumapanduka, mudzaphedwa ndi lupanga. Ine Chauta ndatero.” Taonanitu! Mzinda umene kale udaali wokhulupirika ndi wachilungamo, tsopano ukuchita zadama. Mzinda umene kale udaali ndi anthu aungwiro, tsopano wadzaza ndi anthu opha anzao. Iwe Yerusalemu, unali ngati siliva, koma tsopano wasanduka wopandapake. Unali ngati vinyo wabwino, koma tsopano uli ngati vinyo wosakanizika ndi madzi. Atsogoleri ako apanduka, ndipo amagwirizana ndi mbala. Aliyense amakonda chiphuphu, ndipo amathamangira mphatso. Satchinjiriza ana amasiye, ndipo samvera madandaulo a akazi amasiye. Nchifukwa chake Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, Wamphamvu uja wa Israele, akunena kuti: “Ha! Olimbana nane ndidzaŵatha, adani anga ndidzaŵalipsira. Ndidzatambasula dzanja langa kuti ndilimbane nawe. Ndidzasungunula machimo ako nkuŵachotsa, monga m'mene amachotsera dzimbiri ndi mankhwala. Aweruzi ako ndidzaŵakhazikitsanso ngati pa masiku akale aja. Aphungu akonso ndidzaŵakhazikitsanso ngati poyamba paja. Pambuyo pake iweyo udzatchedwa mzinda waungwiro, mzinda wokhulupirika.” Chauta ndi wolungama, adzaombola Ziyoni. Chauta ndi waungwiro, adzaombolanso anthu olapa amumzindamo. Koma opanduka ndi ochimwa adzaŵaonongera pamodzi, osiya Chauta adzatheratu. Mudzachita nayo manyazi mitengo ya thundu imene inkakusangalatsani, mudzagwetsa nkhope chifukwa cha minda imene mudaipatula. Pakuti mudzafanafana ndi mtengo wa thundu wofota masamba, mudzakhala ngati munda wopanda madzi. Anthu amphamvu adzasanduka ngati udzu wouma, ntchito zao ngati mbaliŵali. Motero anthuwo adzayakira limodzi ndi ntchito zaozo, popanda woti auzimitse motowo. Nazi zinthu zokhudza Yuda ndi Yerusalemu, zimene Yesaya, mwana wa Amozi, adaziwona m'masomphenya. Pa masiku akudzaŵa phiri la Nyumba ya Chauta adzalisandutsa lalitali koposa mapiri ena onse, lidzangoti joo pamwamba pa magomo onse. Mitundu yonse ya anthu idzathamangira ku phiri limenelo. Anthu a mitundu yambiri adzabwera, ndipo adzanena kuti, “Tiyeni tikwere ku phiri la Chauta, ku Nyumba ya Mulungu wa Yakobe. Iye adzatiphunzitsa njira zake, ndipo tidzayenda m'njira zakezo.” Pakutitu nku Ziyoni kumene kudzafumira malangizo akewo, nku Yerusalemu kumene kudzachokera mau a Chauta. Iyeyo adzaweruza pakati pa mitundu ya anthu, adzathetsa kusamvana pakati pa mafuko ambiri. Anthuwo adzasula malupanga ao kuti akhale makasu, ndiponso mikondo yao kuti ikhale mapwitika. Mitundu ya anthu sidzasamulirananso malupanga, sidzaphunziranso zomenyana nkhondo. Inu zidzukulu za Yakobe, tiyeni tiyende m'kuŵala kwa Chauta. Inu Mulungu, mwakana anthu anu, zidzukulu za Yakobe. Dziko ladzaza ndi anthu amatsenga akuvuma, ladzazanso ndi olosa a ku Filistiya. Anthu anu akuchita nao miyambo yachilendo. Dziko la anthu anu nlodzaza ndi siliva ndi golide, ndipo chuma chao nchosatha. Dziko lao nlodzaza ndi akavalo, ndipo magaleta ao ankhondo ndi osaŵerengeka. Dziko lao nlodzaza ndi mafano. Iwo amapembedza mafano opanga ndi manja ao, oumba ndi zala zao zomwe. Nchifukwa chake adzaŵachepetsa ndi kuŵatsitsa. Inu Chauta, musaŵakhululukire! Loŵani m'matanthwe, bisalani m'maenje kuti muthaŵe mkwiyo wa Chauta, muthaŵenso ulemerero wa ufumu wake. Kudzikuza kwa anthu kudzatha, kudzitama kwa anthu kudzaonongedwa. Chauta yekha ndiye adzapatsidwe ulemu tsiku limenelo. Chauta Wamphamvuzonse wakonzeratu tsiku, pamene adzatsitsa onse onyada ndi odzitama, ndipo adzagonjetsa onse amphamvu. Adzadula mikungudza yonse ya ku Lebanoni, italiitali kopambana ina yonse. Adzalikha mitengo yonse ya thundu ya ku Basani. Adzasalaza mapiri onse aatali. Adzafafaniza magomo onse okwera. Adzagwetsa nsanja zonse zazitali. Adzagumula malinga onse olimba. Adzamiza zombo zonse za ku Tarisisi. Adzaononga mabwato onse okongola. Kudzikuza kwa anthu kudzatha, kudzitama kwao konse kudzaonongedwa. Chauta yekha ndiye adzapatsidwe ulemu tsiku limenelo. Mafano onse adzatheratu. Anthu adzathaŵira m'mapanga am'matanthwe ndi m'maenje am'nthaka, kuthaŵa mkwiyo wa Chauta, kuthaŵanso ulemerero wa ufumu wake, pamene Iye adzabwere kudzaopsa dziko lapansi. Tsiku limenelo anthu adzatayira mfuko ndi mileme mafano asiliva ndi agolide, amene adaadzipangira kuti azipembedza. Adzathaŵira m'mapanga am'matanthwe ndi m'ming'alu yam'nthaka, kuthaŵa mkwiyo wa Chauta, kuthaŵanso ulemerero wa ufumu wake, pamene Iye adzabwere kudzaopsa dziko lapansi. Musakhulupirirenso munthu, poti moyo wake sukhalira kutha. Nanga iye nkumuyesanso kanthu ngati! Tsopano Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, ali pafupi kulanda Yerusalemu ndi Yuda chithandizo cha mtundu uliwonse chimene anthu amadalira. Adzachotsa chakudya chonse, adzachotsa madzi onse, anthu amphamvu ndi asilikali ankhondo, aweruzi ndi aneneri, olosa ndi akuluakulu, atsogoleri ankhondo ndi anthu olemekezeka, aphungu ndi amatsenga, ndiponso akatswiri a njirisi. Adzaŵaikira anyamata kuti akhale mafumu ao, ndipo ana amakanda ndiwo adzaŵalamulira. Anthu adzazunzana, aliyense adzazunza mnzake. Anyamata adzachita chipongwe akuluakulu, ndipo anthu achabechabe adzanyoza olemekezeka. Munthu adzagwira mbale wake m'nyumba ya atate ao, nkunena kuti, “Iwe uli nawo mwinjiro, ndiye ukhale mtsogoleri wathu nthaŵi yamavutoyi.” Tsiku limenelo mbale wakeyo adzayankha kuti, “Ine ai toto! Mavuto otereŵa ndilibe mankhwala ake, m'nyumba mwanga momwe ndilibe chakudya kapena chovala. Musaike ine kuti ndikhale mtsogoleri wa anthu.” Zoonadi Yerusalemu akusakazika ndipo Yuda akugwa, chifukwa zokamba ndiponso ntchito za anthu am'menemo nzonyoza Chauta. Salabadako za ulemerero wa Mulungu. Maonekedwe a nkhope zao amaŵatsutsa. Amachimwa poyera ngati m'mene ankachitira anthu a mu Sodomu, sabisa konse. Tsoka kwa iwowo, achita kudziputira okha mavuto. Ngodala anthu omvera Mulungu pakuti zinthu zidzaŵayendera bwino, adzakondwera ndi phindu la ntchito zao. Koma tsoka kwa anthu oipa! Zinthu zidzaŵaipira. Zimene akhala akuchitira anzao zomwezo zidzaŵabwerera. Inu anthu anga, amene akukuponderezani ndi ana chabe, ndipo amene akukulamulani ndi akazi. Aah! Anthu anga, atsogoleri anu akukusokeretsani, akukusokonezerani njira zanu. Tsopano Chauta afuna kuyambapo mlandu, wakonzeka kale kuweruza anthu ake. Chauta akuŵaimba mlandu akuluakulu ndi atsogoleri a anthu ake. Akuŵazenga kuti, “Ndinu amene mwaononga munda wanga wamphesa. Nyumba zanu zadzaza ndi zinthu zolanda kwa amphaŵi. Mukuŵapsinjiranji anthu anga? Chifukwa chiyani mukuŵadyera masuku pamutu amphaŵi?” Akutero Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse. Chauta adati, “Akazi a ku Ziyoni ngodzikuza kwambiri: amayenda makosi ali wee, amayang'ana ndi maso ophika. Amayenda nyang'anyang'a ndi kuliza zigwinjiri zam'miyendo. Nchifukwa chake Ambuye adzatulutsa zipere kumutu kwa akazi a ku Ziyoniwo, tsitsi lao lonse lidzatha phu!” Tsiku limenelo Ambuye adzaŵachotsera zokongoletsera m'miyendo, kumutu ndi m'khosi, maukufu, makoza, ndi nsalu zakumaso, maduku, zigwinjiri, malamba, mabotolo a zonunkhira, zithumwa, mphete, zipini, madelesi apaphwando, makepi, miinjiro, zikwama, akalilole, zovala zabafuta, nduŵira, ndiponso nsalu zam'mapewa. M'malo mwa kununkhira padzakhala kununkha, m'malo mwa lamba adzavala chingwe, m'malo mwa tsitsi lopesa bwino adzakhala ndi mipala, m'malo mwa delesi la mtengo wapatali adzavala chiguduli, m'malo mwa kunyadira kukongola adzachita manyazi. Iwe Yerusalemu, anthu ako aamuna adzaphedwa ndi lupanga, ndipo anthu ako amphamvu adzafera ku nkhondo. Choncho pa zipata zako padzakhala kulira kokhakokha, iweyo udzasakazidwa nkukhala pansi, ukuvimvinizika pa fumbi. Tsiku limenelo akazi asanu ndi aŵiri adzagwira mwamuna mmodzi, nkunena kuti, “Ife tizidya chakudya chathuchathu nkumavala zovala zathu; inu mungotilola tizitchulidwa akazi anu, kuti manyazi aumbeta atichoke.” Tsiku limenelo Chauta adzaphukitsa Nthambi yake imene idzakhala yokongola ndi yaulemerero. Ndipo chipatso cha m'dziko la Israele chidzaŵanyaditsa ndi kuŵapatsa ulemerero onse otsalira. Tsono otsalira ku Ziyoni, amene Mulungu waŵasankha kuti akhale ndi moyo ku Yerusalemu, adzatchedwa oyera. Pamenepo Ambuye adzakhala atasambitsa akazi a ku Ziyoni ndi kuchotsa zonyansa zao, ndipo adzakhala atatsuka magazi amene adakhetsedwa mu Yerusalemu. Adzachita zimenezi ndi mpweya woweruza ndi woyeretsa ndi moto. Tsono masana Chauta adzaika mtambo ndi utsi kuzungulira phiri lonse la Ziyoni, pamwamba pa anthu ake. Usiku adzaika malaŵi a moto oŵala. Pamwamba pa zonse padzakhala ulemerero wa Chauta. Ulemerero wake udzakhala mthunzi wothaŵiramo kutentha kwa masana, udzakhala malo opeweramo mphepo ndi ousiramo mvula. Ntamuimbirako bwenzi langa nyimbo yokamba za wokondedwa wanga ndi munda wake wamphesa. Wokondedwa wanga anali ndi munda wamphesa pa phiri la nthaka yachonde. Adautipula nachotsa miyala yonse, ndipo adaokamo mipesa yabwino kwabasi. Adamanga nsanja pakati pa mundawo, nasema mopondera mphesa m'kati momwemo. Adaayembekeza kuti mundawo udzabala mphesa zabwino, koma ai, udabala mphesa zachabechabe. Ndiye wokondedwa wanga akuti, “Inu amene mumakhala ku Yerusalemu, ndi inu anthu a ku Yuda, ndakupembani, taweruzani pakati pa ine ndi munda wanga wamphesawu. Kodi chilipo chinanso chimene ndidaayenera kuuchitira munda wanga wamphesa, koma sindidachite? Pamene ndinkayembekeza kuti udzabala mphesa zabwino, bwanji udabala mphesa zachabechabe? “Tsopano taimani nkuuzeni zimene ndidzauchite munda wanga wamphesawo. Ndidzazula mpanda wake, ndipo mundawo udzaonongeka. Ndidzagwetsa chipupa chake, ndipo nyama zidzapondapondamo. Ndidzausandutsa tsala, udzakhala wosatengulira ndi wosalimira, ndipo mudzamera mkandankhuku ndi minga ina. Ndidzalamula mitambo kuti isagwetse mvula pamundapo.” Tsonotu munda wamphesawo wa Chauta Wamphamvuzonseyo ndi dziko la Israele, ndipo Ayuda ndiwo mipesa yake yokondweretsa. Iye ankayembekeza ntchito zabwino, koma adangoona kuphana. Ankayembekeza chilungamo, koma adangomva kulira kwa anthu ozunzidwa. Tsoka kwa amene amangokhalira kulumikiza nyumba amene amangokhalira kuwonjezera minda, mpaka kulanda malo onse, kuti dziko lonse likhale la iwo okha. Ndamva Chauta Wamphamvuzonse akulumbira kuti: “Ndithudi, nyumba zambirizo zidzasanduka mainja, nyumba zazikulu zokongolazo zidzakhala zopanda anthu. Munda wamphesa wa mahekitara khumi, vinyo wake adzangodzaza mbiya imodzi. Kufesa madengu khumi a mbeu, zokolola zake zidzangodzaza dengu limodzi.” Tsoka kwa amene amadzuka m'mamaŵa nathamangira chakumwa choledzeretsa, amene amamwa mpaka usiku kufikira ataledzera kotheratu. Amangoimba zeze, pangwe, ng'oma ndi chitoliro, nkumamwa vinyo pa maphwando ao. Koma sasamala ntchito za Chauta, sapenya ntchito za manja ake. Motero anthu anga adzatengedwa ukapolo chifukwa cha kusamvetsa zinthu. Atsogoleri ao olemekezeka adzafa ndi njala, ndipo anthu wamba ochuluka adzafa ndi ludzu. Nchifukwa chake kumanda sikukhuta, kwangoti kukamwa yasa kuti kulandire aliyense. Anthu otchuka a mu Yerusalemu pamodzi ndi anthu wamba ochuluka, adzagweramo ali wowowo, m'kuledzera kwaoko. Munthu aliyense adzatsitsidwa, onse adzachepetsedwa, anthu odzikuza adzaŵachititsa manyazi. Koma Chauta Wamphamvuzonse adzalemekezedwa chifukwa cha chilungamo chake, Mulungu Woyera adzaonetsa kuyera kwake pochita zaungwiro. Tsono anaankhosa adzadya pamenepo ngati pabusa pao, ndipo anaambuzi adzadya m'mabwinja. Tsoka kwa amene amadzikokera machimo ambiri ndi kunama kwao, amene amalephera kudzimasula ku machimo awo. Amanena kuti, “Chauta afulumire, agwire ntchito yake mwamsanga, kuti ntchitoyo tiiwone. Zimene Woyera uja wa Israele afuna kuchita, zichitiketu kuti tizidziŵe.” Tsoka kwa amene zoipa amaziyesa zabwino ndipo zabwino amaziyesa zoipa, amene mdima amauyesa kuŵala, ndipo kuŵala amakuyesa mdima, amene zoŵaŵa amaziyesa zozuna, ndipo zozuna amaziyesa zoŵaŵa! Tsoka kwa amene amadziwona ngati anzeru ndipo amadziyesa ochenjera! Tsoka kwa zidakwa zimene zimaika mtima pa vinyo! Tsoka kwa anthu amene saopa konse kusakaniza zakumwa zaukali! Amalungamitsa wolakwa chifukwa cha chiphuphu nkuipitsa mlandu wa munthu wosalakwa. Nchifukwa chake monga momwe moto umaonongera chiputu, monga momwenso udzu wouma umapsera m'malaŵi a moto, momwemonso muzu wao udzaola, ndipo maluŵa ao adzafota ndi kuuluka ngati fumbi, chifukwa adakana malamulo a Chauta Wamphamvuzonse, adanyoza mau a Woyera uja wa Israele. Nchifukwa chake ukali wa Chauta waŵayakira anthu ake. Iye watambalitsa dzanja lake pa anthuwo kuti aŵakanthe. Mapiri agwedezeka, ndipo mitembo ya anthuwo yangoti mbwee ngati zinyalala pakati pa miseu. Koma ngakhale Mulungu watero, mkwiyo wake sudaleke, dzanja lake lidakali chitambalitsire. Chauta adzapereka chizindikiro kuitana mtundu wa anthu akutali. Adzaŵaitana anthuwo ndi khweru, kuti abwere kuchokera ku mathero a dziko lapansi. Tsono iwo adzabweradi mothamanga kwambiri. Palibe ndi mmodzi yemwe wodzatopa kapena kukhumudwa, kuwodzera kapena kugona. Palibe lamba wam'chiwuno amene adzamasuke, palibe chingwe cha nsapato zao chimene chidzaduke. Mivi yao ndi yakuthwa, mauta ao onse ngokoka, ziboda za akavalo ao nzolimba ngati mwala, magaleta ao ndi aliŵiro ngati kamvulumvulu. Kufuula kwao kuli ngati kubangula kwa mkango, amabangula ngati misona ya mkango, imene imadzuma pogwira nyama, nipita nazo popanda ndi mmodzi yemwe wozipulumutsa. Tsiku limenelo adzaŵakokolola monga momwe mtsinje waukulu umakokololera chilichonse chomwe chili mu njira yake ndi mkokomo wa madzi amphamvu. Ndipo wina kuti ayang'ane dzikolo, adzangoona mdima ndi zovuta. Ngakhale kuŵala kudzasanduka mdima chifukwa cha mitambo. Chaka chimene mfumu Uziya adamwalira, ndidaona Ambuye atakhala pa mpando waufumu wautali ndi wokwezedwa. Mkanjo wao unali wautali kwambiri, kotero kuti udadzaza Nyumba yao yonse. Pamwamba pao padaaimirira Aserafi. Aliyense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi: aŵiri ophimbira kumaso, aŵiri ophimbira mapazi, aŵiri oulukira. Aserafiwo ankafuulirana kuti, “Ngwoyera, ngwoyera, ngwoyera Chauta Wamphamvuzonse, ulemerero wake wadzaza dziko lonse lapansi.” Chifukwa cha kufuulako maziko a zitseko ndi ziwundo adagwedezeka ndipo m'Nyumba ya Chautamo mudangoti utsi pha. Apo ine ndidati: “Tsoka langa ine! Ndatayika. Pakuti ndine munthu wa pakamwa poipa, ndipo ndimakhala pakati pa anthu a pakamwa poipa. Komabe maso anga aona Mfumu, Chauta Wamphamvuzonse.” Pomwepo mmodzi mwa Aserafi aja adaulukira kwa ine, ali ndi khala lamoto m'manja mwake. Khalalo adaalichotsa pa guwa la nsembe ndi mbaniro. Ndipo adandikhudza pakamwa ndi khala lamotolo nati, “Taona, ndakukhudza milomo ndi khalali. Kulakwa kwako kwachotsedwa, machimo ako akhululukidwa.” Kenaka ndidamva mau a Ambuye akuti, “Kodi ndidzatuma yani, ndani adzatipitire?” Apo ndidati “Ndilipo ineyo, tumeni.” Ndipo Ambuyewo adati, “Pita, kaŵauze anthu ameneŵa kuti, ‘Kumva muzimva, koma osamvetsa. Kupenya muzipenya, koma osazindikira.’ Tsono anthu ameneŵa uŵaphe mtima, uŵagonthetse makutu, ndipo uŵatseke m'maso, kuti angaone ndi maso ao, angamve ndi makutu ao, angamvetse ndi mitima yao, kenaka nkutembenuka mtima ndi kuchiritsidwa.” Pamenepo ndidafunsa kuti, “Zimenezo ndi mpaka liti, Inu Ambuye?” Iwo adati: “Mpaka mizinda itasanduka mabwinja, mpaka nyumba zitasoŵa anthu okhalamo, mpaka dziko litasanduka chipululu ndithu. Ine anthuŵa ndidzaŵasamutsira kutali, ndipo dziko lidzakhala thengo. Tsono ngakhale chigawo chachikhumi cha anthu chitsaleko m'dzikomo, nachonso chidzayatsidwa moto. Koma monga mitengo ya muŵanga ndi ya thundu imasiya chitsa akaidula, chonchonso mbeu yoyera ija idzatsalira ngati chitsa chotsala m'dziko.” Pamene Ahazi, mwana wa Yotamu, mdzukulu wa Uziya, anali mfumu ya ku Yuda, Rezini mfumu ya ku Siriya ndiponso Peka mwana wa Remaliya, mfumu ya ku Israele, adaadza ku Yerusalemu, kuti adzathire nkhondo mzindawo, koma sadaugonjetse. Banja lachifumu la ku Yuda litamva kuti dziko la Siriya lagwirizana ndi la Efuremu, mfumu pamodzi ndi anthu ake omwe adanjenjemera, monga m'mene mitengo yam'nkhalango imagwedezekera ndi mphepo. Tsono Chauta adauza Yesaya kuti, “Tenga mwana wako Seari-Yasubu, mupite mukakumane ndi Ahazi kumapeto kwa ngalande yamadzi yochokera ku dziŵe lakumtunda, pa mseu waukulu wopita ku Munda wa Mmisiri Woyeretsa nsalu. Ukamuuze kuti achenjere, akhale phee, asaope, ndipo mtima wake usafooke chifukwa cha ukali woopsa wa Rezini ndi dziko lake la Siriya ndiponso wa Peka mwana wa Remaliya. Ameneŵa ali ngati zongofuka moto. Mfumu ya ku Siriya ndi mfumu ya ku Efuremu apangana kuti akuchiteni choipa. Akunena kuti, ‘Tiyeni tikalimbane ndi dziko la Yuda, tikaliwopse. Tikaligonjetse kuti likhale lathu, ndipo tikalonge ufumu mwana wa Tabeele kumeneko.’ “Komabe zimene akunena Ambuye Chauta ndi izi, akuti, ‘Zimenezo sizidzatheka, sizidzachitika konse. Paja dziko la Siriya limagonera pa likulu lake Damasiko, ndipo Damasiko amagonera pa mfumu yake Rezini. Kunena za Aefuremu, zisanapite zaka 65, adzaonongedwa kotheratu, sadzakhalanso mtundu wa anthu. Dziko la Efuremu limagonera pa likulu lake Samariya, ndipo Samariya amagonera pa mfumu yake Peka. Mukapanda kulimbika pa chikhulupiriro chanu, ndithu simudzalimba konse.’ ” Chauta adalankhulanso ndi Ahazi kudzera mwa mneneri Yesaya kuti, “Upemphe chizindikiro kwa Chauta, Mulungu wako. Chikhale chozama ngati manda kapena chachitali ngati mlengalenga.” Koma Ahazi adati, “Sindidzapempha, ndipo sindidzayesa Chauta ai.” Apo Yesaya adati, “Mumve tsono, inu chidzukulu cha Davide! Kodi sikukukukwanirani kutopetsa anthu, apa mufuna kutopetsa ndi Mulungu wanga yemwe? Nchifukwa chake Ambuye omwe adzakupatsani inu chizindikiro. Onani, namwali uja watenga pathupi ndipo adzabala mwana wamwamuna, mwanayo adzamutcha dzina lake Imanuele. Azidzadya chambiko ndi uchi, mpaka atadziŵa kukana choipa ndi kusankha chabwino. Koma nthaŵi imeneyo isanafike, maiko a mafumu aŵiri amene akukuwopsaniwo, adzakhala atasanduka mabwinja. “Chauta adzafikitsa pa inu, pa anthu anu, ndiponso pa banja la bambo wanu, masiku amavuto oti sadakhalepo kuyambira tsiku limene Efuremu adapatukana ndi Yuda. Ndiye kuti adzafikitsa mfumu ya ku Asiriya.” “Tsiku limenelo Chauta adzalizira khweru Aejipito ndipo adzabwera ambiri ngati ntchentche, zochokera ku mathero a nthambi za mtsinje wa Nailo. Adzaliziranso Aasiriya ndipo adzabwera ambiri ngati njuchi. Onsewo adzafika ndi kudzakhazikika m'zigwa zozama, m'ming'alu yam'matanthwe ndi pa zitsamba zonse zaminga, ndiponso pa mabusa onse. “Tsiku limenelo Ambuye adzalemba wometa wochokera ku tsidya la mtsinje wa Yufurate, ndiye kuti mfumu ya ku Asiriya. Ndi lumo lake adzakumetani tsitsi lakumutu ndi lam'thupi, ndi ndevu zomwe. “Tsiku limenelo mwina munthu adzangosunga ng'ombe yaing'ono yamkaka ndi mbuzi ziŵiri. Komabe adzapeza ndithu mkaka wochuluka, mwakuti munthuyo azidzadya bwino kwambiri. Pakuti aliyense amene adzatsalire m'dzikomo azidzadya chambiko ndiponso uchi. “Tsiku limenelo likadzafika, minda yamphesa yabwino, yomwe ili ndi mitengo yokwana chikwi m'munda uliwonse ndipo mtengo wake ndi masekeli siliva okwana chikwi chimodzi pa mtengo uliwonse, mudzamera a mkandankhuku ndi minga. Anthu adzafika kumeneko kudzachita uzimba ali ndi uta ndi mivi, popeza kuti m'dziko monsemo mudzakhala mkandankhuku ndi minga. Ndipo m'mapiri monse m'mene kale munkalimidwa, anthu sadzafikako, kuwopa mkandankhukuwo ndi mingayo. Malowo adzasanduka odyetserako ng'ombe ndi nkhosa basi.” Chauta adandiwuza kuti, “Tenga cholemberapo chachikulu ndipo ulembepo ndi malembo odziŵika bwino kuti ‘KUSAKAZA-KWAMSANGA-KUFUNKHA-KOFULUMIRA.’ ” Tsono ndidapeza mboni zokhulupirika, wansembe Uriya ndiponso Zekariya mwana wa Yeberekiya, kuti andichitire umboni. Patapita nthaŵi mkazi wanga adaima, nabala mwana wamwamuna. Pamenepo Chauta adandiwuza kuti, “Umutche dzina lakuti KUSAKAZA-KWAMSANGA-KUFUNKHA-KOFULUMIRA. Pakuti mwanayo asanayambe kuitana kuti ‘Ababa’ kapena kuti ‘Amama’, chuma cha Damasiko ndi zofunkha za Samariya zidzatengedwa ndi mfumu ya ku Asiriya.” Chauta adandiwuzanso kuti, “Anthu a dziko ili akana madzi anga a ku Siloamu oyenda mwachifatse, ndipo amakondwerera Rezini ndi mwana wa Remaliya. Nchifukwa chake Ine Ambuye ndidzaŵadzetsera mfumu ya ku Asiriya ndi ankhondo ake kuti adzathire nkhondo Yuda. Adzabwera ngati chigumula cha madzi a mtsinje wa Yufurate osefukira pa magombe ake onse. Adzaloŵa mwamphamvu m'dziko la Yuda, ndipo adzasefukira nadzapitirira mpaka kumayesa m'khosi. Adzachita ngati kutambasula mapiko ake ndi kuphimba dziko lako lonse, iwe Imanuele!” Sonkhanani mwamantha, inu mitundu ina ya anthu, ndipo munjenjemere. Mvetsetsani, inu maiko onse akutali. Valani zankhondo, komabe mudzaonongedwa. Inde, valanidi zankhondo, komabe mudzatha. Chitani upo, koma upowo sudzaphula kanthu. Mupangane zochita, koma zidzalephereka, pakuti Mulungu ali nafe. Chauta adandilangiza mwamphamvu, ndipo adandichenjeza kuti ndisamayenda m'njira ya anthuŵa. Adati, “Usamachita nao zimene anthu ameneŵa amachita, ndipo usamaopa zimene iwowo amaopa, usachite nazo mantha. Chauta Wamphamvuzonse ndiye amene uyenera kumuwona kuti ndi woyera, ndiye amene uyenera kumuwopa, ndiye amene uyenera kuchita naye mantha, ndiye adzakhala ngati malo opatulika. Koma kwa anthu a ku Yuda ndi a ku Israele adzakhala ngati mwala wokhumudwitsa, ndiponso ngati thanthwe logwetsetsa. Kwa anthu a mu Yerusalemu, adzakhala ngati msampha ndi khwekhwe. Ndipo anthu ambiri adzakhumudwapo. Adzagwa nadzathyokathyoka. Adzakodwa mu msampha ndi kugwidwa.” Manga bwino umboniwu ndipo umatepo chimatiro pa mau ameneŵa, pamaso pa ophunzira anga. Ndidzayembekeza Chauta amene akubisira fuko la Yakobe nkhope yake, ndipo ndidzaika chikhulupiriro changa mwa Iye. Onani, ine ndi ana amene Chauta wandipatsa, ndife zizindikiro ndi zidziŵitso kwa Aisraele zofuma kwa Chauta Wamphamvuzonse amene amakhala pa phiri la Ziyoni. Tsono anthu akakuuzani kuti, “Kafunseni kwa olankhula ndi mizimu ndi kwa olosa amene amatulutsa liwu loti psepsepse ndi kumang'ung'udza.” Kodi anthu sayenera kupempha nzeru kwa milungu yao? Kodi sungapite kwa anthu akufa kukapemphera nzeru anthu amoyo, kuti akalandireko mau enieni ndi malangizo? Iyai, amene amalankhula motero, mwa iwo mulibe konse kuŵala. Anthu adzayendayenda m'dziko movutika kwambiri ali ndi njala. Chifukwa cha njalayo, adzakalipa, ndipo adzayang'ana kumwamba ndi kutemberera mfumu yao ndi Mulungu wao. Koma akadzayang'ana pa dziko, adzangoona mavuto okhaokha ndi mdima woopsa ndi wodetsa nkhaŵa. Adzaponyedwa mu mdima wandiweyani. Koma anthu amene anali ndi nkhaŵa, sadzakhalanso otaya mtima. Masiku amakedzana Mulungu adaanyozetsa dziko la Zebuloni ndi la Nafutali, koma kutsogolo kuno adzalisandutsa laulemu dera lonseli, kuyambira ku nyanja yaikulu kuzambwe mpaka kukafika ku dziko la patsidya pa mtsinje wa Yordani, ndiye kuti dziko la Galilea, dziko la anthu a mitundu ina. Anthu amene ankayenda mumdima aona kuŵala kwakukulu. Amene ankakhala m'dziko la mdima wandiweyani, kuŵala kwaŵaonekera. Inu Chauta, mwauchulukitsa mtundu wanu, mwaonjezera kukondwa kwa anthu anu. Iwo akukondwa pamaso panu monga m'mene anthu amakondwera nthaŵi ya masika, monganso m'mene anthu amakondwera pogaŵana zofunkha. Pakuti inu mwathyola goli limene linkaŵalemera, ndodo zimene ankamenyera mapewa ao, ndiponso mikwapulo ya anthu oŵazunza, monga mudaachitira pogonjetsa Amidiyani. Ndithu, nsapato iliyonse ya munthu wankhondo ndi chovala chilichonse chothonyezekera magazi, zidzatenthedwa pa moto ngati nkhuni. Chifukwa mwana watibadwira, mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife. Ulamuliro udzakhala m'manja mwake, ndipo adzamtchula dzina lake lakuti “Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Amuyaya, Mfumu ya Mtendere.” Ulamuliro ndi mtendere wake zidzanka zikukulirakulira. Iye adzakhala pa mpando wa mfumu Davide, ndipo adzakhazikitsa ndi kuchirikiza ufumu wake, pochita zachilungamo ndi zangwiro kuyambira nthaŵi imeneyo mpaka muyaya. Ndi mtima wake wonse Chauta Wamphamvuzonse watsimikiza kuti adzachitadi zimenezi. Ambuye atumiza mau otsutsa Yakobe, mauwo agwa pa Aisraele, zidzukulu zake. Anthu onse, ndiye kuti Aefuremu ndi anthu okhala m'Samariya, adzazimva zotsatira zake za mau ameneŵa. Iwo amalankhula monyada ndi modzikuza kuti, “Ngakhale njerwa zagumuka, ife tidzamanga ndi miyala yosema. Ngakhale mitanda yamkuyu yagwetsedwa, ife tidzaika mitanda yamkungudza m'malo mwake.” Koma Chauta waŵautsira adani, Waŵakhwirizira adaniwo kuti amenyane nawo. Asiriya chakuvuma ndi Afilisti chakuzambwe ayasama kukamwa kuti adye Aisraele. Komabe mkwiyo wa Mulungu sudaŵachoke chifukwa cha zonsezi, ndipo mkono wake uli chisamulirecho kufuna kuŵalanga. Anthuwo sadabwerere kwa Mulungu amene adaŵakantha uja, sadalape ndi kufunafuna Chauta Wamphamvuzonse. Nchifukwa chake Chauta wadula mutu wa Israele pamodzi ndi mchira womwe, nthambi ya kanjedza ndi bango lomwe pa tsiku limodzi. Mutuwo ukutanthauza akuluakulu ndi olemekezeka, mchirawo ukutanthauza aneneri ophunzitsa zabodza. Pakuti amene amatsogolera anthuŵa amaŵasokeza, ndipo otsogoleredwawo amatayika. Nchifukwa chake Ambuye sadzakondwera nawo achinyamata, ndipo sadzaŵachitira chifundo ana amasiye ndi akazi amasiye. Pakuti aliyense ndi wosasamala za Mulungu ndiponso ndi wochimwa. Pakamwa paliponse pamalankhula zopusa. Komabe mkwiyo wa Mulungu sudaŵachoke chifukwa cha zonsezi, ndipo mkono wake uli chisamulirecho kufuna kuŵalanga. Kuipa kwa anthuwo kumayaka ngati moto, moto wake wotentha mkandankhuku ndi minga. Umayatsanso nkhalango ndipo utsi wake umachita kuti toloo ngati mtambo wochindikira. Nchifukwa chake mkwiyo wa Chauta Wamphamvuzonse watentha dziko, ndipo anthu ali ngati nkhuni zosonkhera moto. Palibe munthu wochitira chifundo mbale wake. Ku dzanja lamanja amapeza ndi kudya chakudya, koma osakhuta, ku dzanja lamanzere amapeza ndi kudya chakudya, koma njala ali nayobe. Kwatsala nkumangodyana okhaokha. Amanase akuthira Aefuremu nkhondo, Aefuremu akuthira Amanase nkhondo. Onsewo pamodzi akumenyana ndi Yuda. Komabe mkwiyo wa Mulungu sudaŵachoke chifukwa cha zonsezi, ndipo mkono wake uli chisamulirecho kufuna kuŵalanga. Tsoka kwa amene amapanga malamulo opanda chilungamo, ndi kwa alembi amene amalemba zongovutitsa anzao. Pakutero amapotoza malamulo poweruza amphaŵi mosalungama. Amaŵalanda zoŵayenerera anthu anga osauka, amafunkha za akazi amasiye ndi kubera ana amasiye! Kodi mudzatani pa tsiku lachilango pofika namondwe wochokera kutali? Kodi mudzathaŵira kwa yani kuti akuthandizeni? Nanga chuma chanu mudzachisiya kuti? Kudzatsala nkungozyolika mwamanyazi pakati pa anthu ogwidwa kapena kufa pamodzi ndi ophedwa. Komabe mkwiyo wa Mulungu sudaŵachoke chifukwa cha zonsezi, ndipo mkono wake uli chisamulirecho kufuna kuŵalanga. Chauta akuti, “Tsoka kwa mfumu ya ku Asiriya, mkwapulo wa ukali wanga, ndodo ya mkwiyo wanga. Ndikumtuma kwa mtundu wosasamala za Mulungu, ndipo ndikumlamula kuti apite kwa anthu amene ndaŵakwiyira, kuti akafunkhe ndi kukalanda chuma chao chonse, ndi kuŵaponderezera pansi ngati matope am'miseu.” Koma mfumu ya ku Asiriya sikudziŵa zimenezi ndipo mtima wake sukuganiza choncho. Mtima wake uli pa kuwononga ndi kupulula mitundu yochuluka ya anthu. Iye akuti: “Kodi atsogoleri anga onse ankhondo si mafumu okhaokha? Ine ndagonjetsa mizinda iyi: Kalino, Karikemisi, Hamati, Aripadi. Ndagonjetsanso Samariya ndi Damasiko. Ine ndidakantha mafumu a anthu opembedza mafano, amene mafano ao ndi aakulu kupambana a ku Yerusalemu ndi a ku Samariya. Ndiye ndingalephere kuwononga Yerusalemu pamodzi ndi mafano ake omwe, monga momwe ndidachitira Samariya ndi mafano ake?” Ambuye atamaliza ntchito yao yolanga onse pa phiri la Ziyoni ndiponso ku Yerusalemu, adzalanganso mfumu ya ku Asiriya, chifukwa cha kudzitama kwake ndi kunyada kwake. Pakuti mfumuyo ikuti, “Ndachita zimenezi ndi mphamvu zanga ndiponso ndi nzeru zanga, pakuti kumvetsa nkwanga. Ndachotsa malire a mitundu ya anthu, ndipo ndafunkha chuma chao. Ndaŵatsitsa amene anali pa mipando yaufumu. Dzanja langa lagwira chuma cha mitundu ya anthu, monga momwe munthu amagwirira chisa cha mbalame. Monga momwe anthu amatolera mazira osiyidwa, ndimo m'mene Ine ndidasonkhanitsira dziko lonse lapansi. Ndipo panalibe mbalame ndi imodzi yomwe yoti mapiko phephere-phephere, kapena yoti kukamwa yasa kapena yolira kuti psepsepse.” Koma Chauta akuti: “Kodi nkhwangwa ingathe kudzikuza kupambana munthu woigwiritsa ntchito? Kodi sowo ingathe kudzikuza kupambana munthu woigwiritsa ntchito? Ndiye kukhala ngati kuti mkwapulo ukuzunguza munthu, kapena ndodo yanyamula munthu!” Nchifukwa chake Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, adzatumiza matenda oondetsa kwa ankhondo amphamvu a mfumu ya ku Asiriya. Ndipo mfumuyo kunyada kwake kudzapsa ndi moto wosazimika. Mulungu, Kuŵala kwa Israele, adzakhala ngati moto. Mulungu, Woyera Uja wa Israele, adzakhala ngati malaŵi a moto. Motowo udzaŵatentha ndi kuŵapsereza ngati minga ndi mkandankhuku pa tsiku limodzi. Adzaononga nkhalango yaikulu ndi nthaka yachonde. Zidzaonongeka m'kati ndi kunja kwake, ndipo zidzakhala ngati munthu wodwala amene akuwonda. Mitengo yotsalira yam'nkhalangomo idzakhala yochepa kwambiri, yoti ndi mwana yemwe nkuiŵerenga. Tsiku limenelo otsalira a ku Israele, opulumuka a m'banja la Yakobe, sadzadaliranso anthu amene adaŵakantha, koma ndithu adzadalira Chauta, Woyera Uja wa Israele. Otsalira adzabwerera, otsalira a m'banja la Yakobe, adzabwereradi kwa Mulungu wamphamvu. Iwe Israele, ngakhale anthu ako achuluke ngati mchenga wakunyanja, otsalira oŵerengeka okha ndiwo adzabwerere. Chiwonongeko chalamulidwa, chidzaonetsa chilungamo chosefukira. Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, adzaononga ndithu dziko lonse monga momwe adalamulira. Nchifukwa chake Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, akunena kuti, “Inu anthu anga okhala ku Ziyoni, musaŵaope Aasiriya pamene akukanthani ndi ndodo, nakumenyani ndi zibonga zao, monga m'mene Aejipito ankachitira. Patsala pang'onong'ono kuti uthe mkwiyo wanga pa inu, koma ndidzaŵakwiyira iwonso mpaka kuŵaononga. Ine, Chauta Wamphamvuzonse, ndidzaŵakwapula monga momwe ndidakwapulira Amidiyani ku thanthwe la Orebu. Ndi ndodo yanga ndidzaŵalanga, monga momwe ndidalangira Aejipito panyanja paja. Tsiku limenelo ndidzakusanjulani katundu wa Aasiriya pa mapewa anu, ndi goli lao m'khosi mwanu, golilo lidzathyoka chifukwa cha kunenepa.” Adani aja akudza afika ku Aiyati. Apyola ku Migironi, aikiza katundu wao ku Mikimasi. Adzera pa mpata uja, nagona ku Geba usiku. Anthu a ku Rama akunjenjemera, a ku Gibea, mzinda wa Saulo, athaŵa. Lirani mokweza, inu anthu a ku Galimu! Tcherani khutu, inu anthu a ku Laisa! Yankhani, inu a ku Anatoti. Anthu a ku Madimena akuthaŵa, a ku Gebimu akubisala. Lero lomwe lino adaniwo adzaima ku Nobu, adzagwedeza mikono yao kuwopseza anthu a ku phiri la Ziyoni, phiri la Yerusalemu. Koma Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, adzaŵadula ngati nthambi za mtengo. Akuluakulu adzagwetsedwa, odzikweza adzatsitsidwa. Chauta adzaŵadula monga momwe anthu amadulira ndi nkhwangwa mitengo ya m'kati mwa nkhalango. Iwo adzagwa monga momwe imagwera ngakhale mitengo yaikulu ya ku Lebanoni. Nthambi idzaphuka patsinde pa Yese, ndipo mphukira idzatuluka ku mizu yake. Mzimu wa Chauta udzakhala pa Iye, mzimu wopatsa nzeru ndi kumvetsa, mzimu wopatsa uphungu ndi mphamvu, mzimu wopatsa kudziŵa zinthu ndi kuwopa Chauta. Ndipo kuwopa Chauta ndiye chidzakhale chinthu chomkondweretsa. Sadzaweruza potsata zooneka pamaso, kapena kugamula mlandu potsata zakumva. Koma amphaŵi adzaŵaweruza mwachilungamo, ndipo anthu otsika a pa dziko lapansi adzaŵagamulira mlandu wao mosakondera. Mau ochokera m'kamwa mwake adzakhala ngati ndodo yokanthira ochimwa, atalamula iyeyo anthu oipa adzaphedwa. Chilungamo chidzakhala ngati lamba wake, ndipo kukhulupirika, ngati chomangira m'chiwuno mwake. Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwanawankhosa, kambuku adzagona pansi pamodzi ndi mwanawambuzi, mwanawang'ombe ndi mwanawamkango adzadyera limodzi, mwana wamng'ono nkumaziŵeta zonsezo. Ng'ombe yaikazi ndi chimbalangondo zidzadya pamodzi, ndipo ana ao adzagona pamodzi. Mkango udzadya udzu ngati ng'ombe. Mwana woyamwa adzaseŵera pa dzenje la mamba, ndipo mwana woleka kuyamwa adzapisa dzanja lake ku funkha la mphiri, osalumidwa. Sipadzakhala chilichonse chopweteka kapena choononga pa phiri lopatulika la Mulungu. Ndipo anthu a pa dziko lonse lapansi adzakhala odzaza ndi nzeru ya kudziŵa Chauta, monga nyanja imadzazira ndi madzi. Tsiku limenelo mfumu yatsopano yochokera ku banja la Davide idzakhala chizindikiro kwa anthu a mitundu yonse. Onse adzasonkhana kwa iye, ndipo malo ake okhalapo adzakhala aulemerero. Tsiku limenelo Ambuye adzatambalitsa dzanja lake kachiŵiri kuti aombole anthu ake otsalira ku Asiriya, ku Ejipito, ku Patirosi, ku Etiopiya, ku Elamu, ku Sinara, ku Hamati ndi pa zilumba za m'nyanja yamchere. Adzakwezera mitundu ya anthu mbendera, adzasonkhanitsa otayika a ku Israele ndi obalalika a ku Yuda kuchokera ku mbali zonse zinai za dziko lapansi. Nsanje ya Efuremu idzatha, ndipo osautsa Yuda adzaonongeka. Efuremu sadzadukidwa ndi Yuda, ndipo Yuda sadzavuta Efuremu. Koma Yuda ndi Efuremu adzathira nkhondo pa Afilisti kuzambwe, ndipo onsewo pamodzi adzalanda zinthu za anthu akuvuma. Adzalimbana ndi Aedomu ndi Amowabu, ndipo Aamoni adzaŵagonjera. Ndipo Chauta adzaphwetsa kotheratu mwendo wa nyanja yofiira ya ku Ejipito. Adzatambalitsa dzanja lake ndipo adzaombetsa mphepo yotentha pa mtsinje wa Yufurate. Mtsinjewo udzagaŵikana m'timitsinje tisanu ndi tiŵiri, kuti anthu aoloke pouma. Padzakhala mseu waukulu woti ayendepo otsalira ku Asiriya aja, monga m'mene panaliri mseu waukulu woyendapo Aisraele pochoka ku Ejipito. Tsiku limenelo aliyense mwa inu adzati: “Ndikukuthokozani Inu Chauta, pakuti ngakhale mudaandipsera mtima, mkwiyo wanu udaleka, ndipo mwandilimbitsa mtima. “Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa. Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.” Mudzakondwera pokatunga madzi m'zitsime za chipulumutso. Tsiku limenelo mudzati: “Thokozani Chauta, tamandani dzina lake. Mulengeze ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu, mulalike kuti dzina lake ndi lopambana. “Imbirani Chauta nyimbo zotamanda, pakuti wachita zazikulu. Zimenezi zidziŵike pa dziko lonse lapansi. Fuulani ndi kuimba mokondwa, inu anthu a ku Ziyoni, pakuti Woyera Uja wa Israele ndi wamkulu pakati panu.” Nawu uthenga wonena za Babiloni umene Yesaya, mwana wa Amozi, adalandira kwa Mulungu. Kwezani mbendera yankhondo pa phiri loti see. Muŵafuulire ankhondo ndi kuŵakodola kuti adzaloŵe pa zipata za mzinda. Ine Mulungu mwini wake ndapereka malamulo kwa anthu anga opatulika. Ndasonkhanitsa ankhondo amphamvu, amene amakondwerera kupambana kwanga, kuti akhale zida zanga zolangira amene ndimaŵakwiyira. Tamvani phokoso kumapiriku! Likumveka ngati phokoso la chinamtindi cha anthu. Imvani chiwawa m'maufumu! Ndiye ngati mitundu ya anthu ikusonkhana pamodzi. Chauta Wamphamvuzonse akukhazika ankhondo ake mokonzekera kumenya nkhondo. Iwowo akuchokera ku maiko akutali, ku malekezero a dziko. Ndiye kuti Chauta wanyamula zida zake zija mokwiya, akubwera kuti adzaononge dziko lonse lapansi. Lirani kwamphamvu pakuti tsiku la Chauta layandikira. Likubwera ndi chiwonongeko chochokera kwa Mphambe. Tsono manja onse adzafooka, ndipo mtima wa munthu aliyense udzachokamo. Onse adzada nkhaŵa, adzavutika ndi kumva zoŵaŵa, zoŵaŵa zake zonga zimene amazimva mkazi pochira. Azidzayang'anana mwamantha, nkhope zao zidzagwa ndi manyazi. Zoonadi, tsiku la Chauta likudza, tsiku lopanda chisoni, laukali ndi lamkwiyo. Chauta akubwera kuti asandutse dziko lapansi chipululu ndi kuwononga anthu ochimwa am'menemo. Nyenyezi zonse zakumwamba sizidzaonetsanso kuŵala. Dzuŵa lidzada potuluka, ndipo mwezi sudzaŵala konse. Chauta akuti, “Ndidzalanga anthu a dziko lapansi chifukwa cha kuipa kwao, ndidzalanga oipa chifukwa cha kuchimwa kwao. Ndidzathetsa kunyada kwa odzikuza ndipo ndidzatsitsa kudzitukumula kwa anthu ankhanza. Anthu ndidzaŵasandutsa osapezekapezeka kuposanso m'mene aliri golide wangwiro, mtundu wa anthu udzakhala wosoŵa ngati golide wa ku Ofiri. Tsono ndidzagwedeza mlengalenga, ndipo dziko lapansi lidzachoka pa maziko ake. Zonsezi zidzachitika chifukwa cha ukali wa Ine Chauta Wamphamvuzonse pa tsiku la mkwiyo wanga woopsa. Choncho munthu aliyense adzabwerera kwa anthu akwao, aliyense adzathaŵira ku dziko lake, ngati mbaŵala zothaŵa anthu auzimba kapenanso ngati nkhosa zopanda wozikusa. Aliyense amene adzapezeke adzabayidwa chipyoza. Aliyense amene adzagwidwe adzaphedwa ndi lupanga. Ana ao akhanda adzatswanyidwa iwo akuwona. M'nyumba mwao mudzafunkhidwa, ndipo akazi ao adzaŵachimwitsa mwakhakhamizo. “Ine Chauta ndidzadzutsa Amedi kuti amenyane ndi Ababiloni. Iwo safuna siliva ndipo sakondwa ndi golide. Adzapha anyamata ndi mauta ao. Sadzachitira chifundo ana. Mitima yao siidzamva chisoni ndi ana akhanda omwe. Babiloni ufumu wake ndi waulemerero kuposa maufumu ena onse, ndipo anthu ake amaunyadira. Koma Ine Chauta ndidzaononga mzinda wa Babiloniwo monga ndidaonongera Sodomu ndi Gomora pa nthaŵi imene ndidagonjetsa mizindayo. Anthu sadzakhalamonso kapena kukhazikikamo pa mibadwo yonse. Mluya aliyense woyendayenda sadzamangako hema kumeneko, abusa sadzaŵetako ziŵeto zao kumeneko. Koma nyama zakuthengo ndizo zimene zidzakhale kumeneko, nyumba zake zidzadzaza ndi akadzidzi. Kuzidzayendayenda nthiŵatiŵa, ndipo atonde akuthengo azidzavinavinako. M'nsanja zake muzidzalira afisi, m'nyumba zake zaufumu zokongola muzidzalira nkhandwe. Nthaŵi yake yayandikira, ndithu masiku ake ali pafupi kutha.” Chauta adzachitira chifundo a m'banja la Yakobe, adzasankhanso Aisraele ndi kuŵalola kuti akhalenso m'dziko lao. Akunja adzabwera kudzakhala nao ndi kuphatikira ku banja la Yakobe. Anthu a mitundu ina adzaperekeza Aisraele ku dziko limene Chauta adaŵapatsa. Kumeneko anthuwo adzakhala otumikira Aisraele ngati akapolo ndi adzakazi. Aisraele adzagwira ukapolo anthu amene kale adaali ambuyao ndi kumalamulira anthu amene kale ankaŵazunza. Chauta adzakupumitsani ku zoŵaŵa ndi mavuto, ndiponso ku ntchito yakalavulagaga imene anthu ankakugwiritsani. Motero mudzanyodola mfumu ya ku Babiloni, mudzati, “Watha bwanji wopsinja uja? Kwatha bwanji kudzikuza kwake kuja? Chauta wathyola mkwapulo wa anthu oipa, wasakaza ndodo yaufumu ya olamulira. Iwowo ankakantha mitundu ya anthu mokwiya pomaŵamenya kosalekeza. Ankalamulira mitundu ya anthu mwaukali ndi kumaŵazunza kosalekeza. Dziko lonse lapansi lapumula, tsopano lakhala bata, ndipo anthu akuimba mokondwa. Mitengo ya paini ikukondwerera kugwa kwa Babiloni. Mikungudza ya ku Lebanoni ikuti, ‘Chigwetsedwere chako pansi, mfumu iwe, palibe wina amene adabwera kudzatigwetsa.’ “Kumanda kwatekeseka kuti kukulandire podzafika iwe mfumu ya ku Babiloni. Mandawo adzutsa mizimu ya anthu akufa kuti ikulonjere iwe, adzutsa mizimu ya onse amene adaali atsogoleri pa dziko lapansi. Akuŵaimiritsa pa mipando yao yaufumu onse amene adaali mafumu a mitundu ya anthu. Onsewo adzalankhula, ndipo adzakuuza kuti: ‘Iwenso watheratu mphamvu monga ife! Tsopano tafanana.’ Ulemerero wako, pamodzi ndi nyimbo za pa azeze ako, zonse zatha, waloŵa nazo m'manda. Bedi lako ndi mphutsi, chofunda chako ndi nyongolotsi. “Wagwa pansi bwanji kuchoka kumwamba, iwe Nthanda, mwana wa Mbandakucha? Wagwetsedwa pansi bwanji, iwe amene unkagonjetsa mitundu ya anthu? Mumtima mwako unkati, ‘Ndidzakwera mpaka kumwamba. Ndidzakhazika mpando wanga waufumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu. Ndidzakhala pampandopo pa phiri la kumpoto kumene imasonkhanako milungu yonse. Ndidzakwera pamwamba pa mitambo, ndidzafanafana naye Wopambanazonse.’ Koma watsitsidwa m'manda, pansi penipeni pa dzenje. “Anthu akufa akakuwona azidzakupenyetsetsa nkuyamba kulingalira za iwe kuti, ‘Kodi uyu si munthu uja ankanjenjemeretsa dziko lapansi, ndi kugwedeza maufumu? Kodi si ameneyu uja adasandutsa dziko lapansi chipululu ndi kugwetsa mizinda, ndipo sankalola kuti anthu ogwidwa abwerere kwao?’ Mafumu onse a mitundu ya anthu akugona mwaulemerero aliyense m'manda akeake. Koma iwe watayidwa kunja kwa manda ako ngati nthambi yoola ndi yonyansa. Mtembo wako waphimbidwa ndi ophedwa amene adabayidwa ndi lupanga, naponyedwa m'dzenje lamiyala. Udzakhala ngati mtembo woponderezedwa. “Sudzaikidwa nao m'manda mwaulemerero, chifukwa chakuti waononga dziko lako, wapha anthu ako. “Zidzukulu za anthu ochita zoipa zisadzakumbukike mpang'ono pomwe. Mukonzekere kupha ana aamuna a mfumuyi, chifukwa cha kulakwa kwa atate ao, kuwopa kuti angadzuke ndi kulanda dziko lapansi ndi kulidzaza dziko lonselo ndi mizinda.” Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Ndidzauthira nkhondo mzinda wa Babiloni. Ndidzathetseratu dzina lake ndi onse otsaliramo. Sipadzapulumuka ana ndi zidzukulu zomwe. Ndatero Ine Chauta. Mzindawo ndidzausandutsa dambo lamatope ndi malo okhalamo akanungu. Ndidzausesa ndi tsache lofafaniza zonse zotsala. Ndatero Ine Chauta Wamphamvuzonse.” Chauta Wamphamvuzonse walumbira kuti, “Monga momwe ndaganizira, zidzachitikadi choncho, ndipo monga momwe ndatsimikizira zidzakhala momwemo ndithu. “Ndidzaŵaononga Aasiriya m'dziko langa, ndipo ndidzaŵapondereza ndi mapazi pa mapiri anga. Tsono anthu anga ndidzaŵavula goli limene Aasiriya adaŵaveka, ndidzaŵachotsera katundu wolemetsa pa mapewa ao. “Zimenezi ndizo zimene ndagamula kuti zidzachitike pa dziko lonse lapansi. Ndatambalitsa dzanja langa kuti ndilange anthu a mitundu yonse.” Chauta Wamphamvuzonse ndiye watsimikiza kuti zimenezi zichitike, nanga ndaninso angathe kumletsa? Dzanja lake nlotambalitsa, nanga ndaninso angalibweze? Chaka chimene mfumu Ahazi adafa, padamveka ulosi uwu: “Musakondwe inu anthu a ku Filistiya, poona kuti adatha Aasiriya amene adaali ngati ndodo yokumenyani. Mu mtundu wa njoka wamba mudzatuluka mphiri, ndipo mu mtundu wa mphiriyo mudzatuluka chinjoka chaliŵiro chaululu. “Osauka zedi adzapeza chakudya, amphaŵi adzakhala pabwino. Koma mtundu wanu Afilistinu ndidzauwononga ndi njala, ndi otsalira omwe ndidzaŵapha. “Lirani kwamphamvu inu apachipata! Pemphani chithandizo mofuula, inu amumzinda! Njenjemerani ndi mantha nonse Afilisti! Onani fumbi likuchita kuti kodoo kuchokera kumpoto, ndipo mwa ankhondo akubwerawo palibe wamantha.” Kodi tidzaŵayankhanji amithenga a ku Filistiyawo? Tidzati, “Chauta adakhazikitsa kale Ziyoni, ndipo mu mzinda umenewu anthu ake ozunzika amapeza populumukira.” Nawu ulosi wonena za Mowabu: Chifukwa chakuti mzinda wa Ari waonongedwa usiku umodzi wokha, dziko la Mowabu lagwa. Chifukwa chakuti mzinda wa Kiri waonongedwa usiku umodzi wokha, dziko la Mowabu lagwa. Anthu a ku Diboni akukwera ku nyumba ya milungu yao, akukwera ku akachisi ao kukalira. Anthu a ku Mowabu akulira mzinda wa Nebo ndi wa Medeba. Mutu uliwonse wametedwa mpala, ndevu zonse zametedwa. M'miseu akuvala ziguduli, pamadenga ndi m'mabwalo aliyense akulira kwamphamvu, misozi ili pupupu. Anthu a ku Hesiboni ndi ku Eleale akulira mofuula. Mau ao akumveka mpaka ku Yahazi. Nchifukwa chake asilikali a ku Mowabu akulira mofuula, ataya mtima. Inenso ndikulira Mowabu. Anthu ake othaŵa nkhondo akuthaŵira ku Zowari, ku Egilati-Selisiya. Akupita nalira ku chikweza cha Luhiti, akulira mosweka mtima pa mseu wopita ku Horonaimu. Ku mtsinje wa Nimurimu madzi adaphwa, udzu udauma, msipu udafota, palibenso chomera chobiriŵira. Nchifukwa chake anthu akuthaŵa atanyamula chuma chao. Afuna kuwoloka nacho Chigwembe cha Misondodzi. Kulira kwao kukumveka ku dziko lonse la Mowabu, kukumveka kuchokera kumpoto ku Egilaimu mpaka kumwera ku Beerelimu. Madzi a ku Diboni asakanizika ndi magazi, komabe ndidzafikitsa zovuta zina zambiri pa Diboni. Ndidzafikitsa mkango woti udzagwire aliyense wopulumuka ku Mowabu, ndiponso aliyense wotsalira m'dzikomo. Amowabu atumiza mphatso ya mwanawankhosa kwa wolamulira dziko. Iwo achokera ku mzinda wa Sela, adzera njira ya chipululu mpaka kukafika ku phiri la Ziyoni. Monga momwe mbalame zimaulukira uku ndi uku akazimwaza m'chisa, momwemonso akazi a ku Mowabu akuyendayenda ku madooko a Arinoni. Akuuza anthu a ku Yuda kuti, “Mutiwuze chochita, gamulani zoti tichite. Pamene dzuŵa lili pa liwombo, mutipatse mthunzi wabii ngati mdima. Mutibise ife anthu opirikitsidwa, musatipereke ife anthu othaŵa nkhondo. Othaŵa nkhondo a ku Mowabu azikhala pakati panu. Mukhale populumukira pao kwa woononga uja.” Nthaŵi ikudza pamene kupsinja sikudzakhalaponso, kuwononga kudzaleka, ndipo amene amaŵapondereza adzachoka m'dzikomo. Pamenepo mpando wachifumu udzakhazikitsidwa mwachikondi, mmodzi mwa zidzukulu za Davide adzakhalapo mokhulupirika. Iyeyo poweruza adzatsata zachilungamo, ndipo adzalimbikira kuchita zaungwiro. Anthu a ku Yuda akunena kuti, “Kudzikuza kwa Amowabu takumva, adadzikuza kwambiri. Kudzitukumula kwao, kunyada kwao, kunyodola kwao ndi kudzitama kwao, zonse nzachabechabe.” Nchifukwa chake alekeni Amowabu alire kwambiri, onsewo alire fuko lao, Alire motaya mtima chifukwa cha makeke amphesa amene ankadya ku Kiri-Haresefi. Paja minda ya ku Hesiboni idaguga, yatha pamodzi ndi minda yamphesa ya ku Sibima. Mphesa zake zinkaledzeretsa olamulira anthu a mitundu ina. Kale nthambi zake zinkafika mpaka ku Yazere ndi ku chipululu, ndiponso mpaka kutsidya kwa nyanja. Nchifukwa chake ndikulira monga m'mene akulirira anthu a mu mzinda wa Yezere chifukwa cha minda yamphesa ya ku Sibima. Inu anthu a ku Hesiboni ndi Eleale ndikukunyowetsani misozi chifukwa choti mwalephera kupeza zokolola, kaamba ka nkhondo imene yaononga zonse. Kukondwa ndi kusangalala kwalekeka ku minda yadzinthu. Nyimbo sizikuimbidwa, palibenso kufuula m'minda yamphesa. Palibe wopsinya vinyo mopondera mphesa, kufuula kwachimwemwe kwa nthaŵi yotchera mphesa kwalekeka. Nchifukwa chake moyo wanga ukulira ngati pangwe, kulira Mowabu, mtima wanga ukubuula chifukwa cha kuwonongeka kwa Kiriheresi. Ngakhale Amowabu akudzipereka pakupita ku akachisi ao namakapemphera mpaka kutopa, zimenezo sizidzaŵapindulira kanthu. Mau ameneŵa ndiwo amene adalankhula Chauta kalekale kunena za Mowabu. Koma tsopano akunena kuti, “Zisanathe zaka zitatu, potsata m'mene amaŵerengera munthu waganyu, ulemerero wa Mowabu udzakhala utatheratu. Chigulu chachikulu cha anthu ake chidzaonongeka, ndipo opulumukapo adzakhala ochepa ndi ofooka.” Nawu ulosi wonena za Damasiko: “Mzinda wa Damasiko sudzakhalanso mzinda, koma udzasanduka bwinja. Mizinda ya ku Siriya idzakhala yopanda anthu mpaka muyaya. Idzasanduka podyera ziŵeto zimene zizidzagonako popanda wina woziwopsa. Ku Efuremu sikudzakhalanso linga, ndipo ku Damasiko sikudzakhalanso ufumu. Otsalira a ku Siriya adzachotsedwa ulemu monga anthu a ku Israele,” akutero Chauta Wamphamvuzonse. “Tsiku limenelo ulemerero wa Yakobe udzachepetsedwa, ndipo chuma chake chidzasanduka umphaŵi. Israele adzakhala ngati munda watirigu umene adatsiriza kukolola. Adzakhalanso ngati munda wa m'chigwa cha Refaimu, anthu atatha kukunkha ngala za tirigu. Ochepa okha adzatsalako, monga pogwedeza mtengo wa olivi, zimatsalako ndithu zipatso ziŵiri kapena zitatu pa nthambi ya pamwamba penipeni, kapenanso zinai kapena zisanu pa nthambi zam'munsi,” akutero Chauta, Mulungu wa Israele. Tsiku limenelo anthu adzayang'ana Mlengi wao, ndipo adzatembenukira kwa Woyera uja wa Israele, kufuna thandizo. Sadzakhulupiriranso maguwa amene iwo omwe adamanga, kapenanso kudalira zimene adapanga ndi manja ao, ngakhale mafano ofanizira Asera kapena maguwa ofukizapo lubani. Tsiku limenelo mizinda yamphamvu ya Aisraele idzasiyidwa monga mizinda ya Aamori ndi ya Ahivi imene anthu adaaisiya pothaŵa Aisraelewo. Ndipo idzakhala mabwinja. Inu Aisraele, mwaiŵala Mulungu Mpulumutsi wanu, simudamkumbukire Iye amene ndiye thanthwe lokupulumutsani. M'malo mwake, mumabzala mbeu zabwino, kubzalira milungu yachilendo, Mumati zikule tsiku lomwe mwabzalalo, mumati zituluke maluŵa m'maŵa momwe mwazibzalamo, komabe zimene mudzakololezo zidzatha pa tsiku lamavuto, ndipo mazunzo ake adzakhala osatha. Ha, anthu a mitundu yambiri akusokosa kwambiri! Phokoso lao lili ngati kukokoma kwa nyanja! Ha, lumbwe la anthu a mitundu ina, likusokosa ngati madzi amphamvu! Ankhondo a mitundu ina akubwera ndi mkokomo ngati wa madzi ambiri. Koma Mulungu akuŵadzudzula, ndipo iwo adzathaŵira kutali. Adzapirikitsidwa ngati mankhusu ouluka ndi mphepo pa mapiri, ngati fumbi la kamvulumvulu namondwe asanayambe. Pa nthaŵi yamadzulo ndi oopsa! Koma kusanache, onse azimirira. Umu ndimo m'mene zidzaŵachitire anthu otilanda zathu. Limeneli ndilo tsoka la anthu otibera zinthu zathu. Tsoka kwa anthu okhala ku dziko la patsidya pa mitsinje ya Etiopiya! Kumeneko kumamveka mkokomo wa mapiko. Kuchokera ku dzikolo amatuma akazembe pa mtsinje wa Nailo m'mabwato agumbwa omangoyandama pa madzi. Tsono pitani inu amithenga aliŵiro kwa mtundu wa anthu ataliatali ndi a khungu losalala, oopedwa ndi anthu akufupi ndi akutali omwe, mtundu wamphamvu ndi wogonjetsa mitundu ina, anthu amene dziko lao nlodukanadukana ndi mitsinje. Inu nonse anthu a pa dziko lapansi, inu amene mumakhala pansi pano, pamene mbendera yakwezedwa pa mapiri, muyang'ane! Lipenga likamalira, mumve! Pakuti Chauta adandiwuza kuti, “Kumene ndili Ineko, ndidzangoyang'ana pansi mwakachetechete, monga m'mene dzuŵa limaŵalira nthaŵi yotentha, monganso m'mene amagwera mame usiku pa nthaŵi yakholola.” Anthu asanayambe kukolola, maluŵa atayoyoka ndipo mphesa zitayamba kupsa, Iye adzadula mphukira ndi chigwandali, ndipo adzasadza nthambi zotambalala. Mitembo ya ankhondowo adzasiyira mbalame zam'mapiri zodya nyama, ndiponso zilombo zakuthengo. Mbalame zidzaidya pa nthaŵi ya chilimwe, ndipo zilombo zakuthengo zidzaidya pa nthaŵi ya chisanu. Pa nthaŵi imeneyo anthu adzabwera ndi zopereka kwa Chauta Wamphamvuzonse. Anthu ake adzakhala aatali ndi a khungu losalala, oopedwa ndi anthu akufupi ndi akutali omwe, mtundu wamphamvu ndi wogonjetsa mitundu ina, anthu amene dziko lao ndi lodukanadukana ndi mitsinje. Zoperekazo adzabwera nazo ku phiri la Ziyoni kumene anthu amapembedza Chauta Wamphamvuzonse. Nawu ulosi wonena za Ejipito. Chauta wakwera pa mtambo wothamanga, akupita ku Ejipito. Mafano a ku Ejipito adzanjenjemera pamaso pake, ndipo Aejipitowo mitima yao idzachokamo ndi mantha. Tsono Ine ndidzautsa Aejipito kuti amenyane okhaokha. Ndipo adzamenyana, mbale ndi mbale wake, mnansi ndi mnansi wake, mzinda ndi mzinda unzake, ndiponso ufumu ndi ufumu unzake. Ndidzalepheretsa zolinga za Aejipito mwakuti adzataya mtima. Tsono adzapempha nzeru kwa mafano, amaula, olankhula ndi mizimu, ndiponso anyanga. Ndidzapereka Aejipito kwa wolamulira wankhalwe. Ndipo mfumu yoopsa ndiyo idzaŵalamulira, akutero Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse. Madzi a mtsinje wa Nailo adzaphwa, ndipo mtsinjewo udzauma kuchita kuti gwaa. Ngalande zake zizidzanunkha, ndipo mphanda za mtsinjewo ku Ejipito zidzayamba kuchepa kenaka nkuuma. Bango ndi mlulu zidzafota, ndipo zomera zonse za m'mphepete mwa Nailo ndi ku mathiriro ake, zidzafa. Zonse zobzalidwa m'mbali mwa Nailo zidzauma, zidzauluzika, zosaonekanso. Asodzi adzadandaula ndi kulira. Onse amene amaŵedza mu mtsinje wa Nailo adzamva chisoni. Onse amene amaponya khoka m'madzi adzalira. Anthu ogwira ntchito yopota thonje, ndiponso anthu oomba nsalu zoyera, adzataya mtima. Akatswiri opanga nsalu adzangoti kakasi, ndipo anthu ogwira ntchito yolipidwa adzangoti m'nkhongono zii. Akalonga a mu mzinda wa Zowani ndi zitsilu. Aphungu anzeru a Farao amalangiza zopusa. Kodi mungathe kumuuza bwanji Farao kunena kuti, “Ine ndine mmodzi mwa anthu anzeru, wophunzira wa mafumu akale?” Iwe Farao, anzeru ako ali kuti? Abwere kuno msanga kuti akudziŵitse zimene Chauta Wamphamvuzonse akunena zotsutsa Ejipito. Akalonga a mu mzinda wa Zowani asanduka zitsilu, ndipo akalonga a ku Memfisi anyengedwa. Amene ali atsogoleri a Aejipito alisokeza dziko lao. Chauta waŵasokoneza Aejipito. Iwo akuchita dzandidzandi pa ntchito zao zonse, ngati chidakwa choterereka pa masanzi ake omwe. Ndipo palibe wina aliyense mu Ejipito amene angachitepo kanthu, wolemera kapena wosauka, wotchuka kapena munthu wamba. Tsiku limenelo Aejipito adzakhala ngati akazi, adzanjenjemera ndi kuchita mantha, akadzaona Chauta Wamphamvuzonse akusamula dzanja kufuna kuŵalanga. Dziko la Yuda lidzaopsa dziko la Ejipito. Ndipo nthaŵi zonse Aejipito akadzamva za Yuda, adzaopsedwa chifukwa cha zimene Chauta Wamphamvuzonse afuna kuŵachita Aejipitowo kudzera mwa Yudayo. Tsiku limenelo ku dziko la Ejipito kudzakhala mizinda isanu yolankhula Chihebri, ndipo anthu ake adzalumbira kwa Chauta Wamphamvuzonse kuti adzamtumikira. Umodzi mwa mizindayo udzatchulidwa “Mzinda wa Dzuŵa.” Tsiku limenelo m'kati mwa dziko la Ejipito mudzakhala guwa la Chauta, ndipo kufupi ndi malire adzaimikirako Chauta mwala wachikumbutso. Zimenezo zidzakhala umboni wozindikiritsa kuti Chauta Wamphamvuzonse alimo m'dziko la Ejipito. Aejipito akadzalira kwa Chauta pa zovuta zao, Iye adzatuma mpulumutsi kuti aŵateteze ndi kuŵapulumutsa. Tsono Chauta adzadziwulula kwa Aejipito, ndipo tsiku limenelo Aejipitowo adzadziŵa Chauta. Adzapembedza Chauta potsira nsembe ndi kupereka zopereka. Adzachita malonjezo aakulu kwa Chauta ndipo adzachitadi zimene adalonjezazo. Ngakhale Chauta adzaŵalange Aejipito dzolimba, adzaŵalanga inde, koma pambuyo pake adzaŵachiritsa. Iwo adzatembenukira kwa Chauta, ndipo Iye adzaŵamvera ndi kuŵachiritsa. Tsiku limenelo kudzakhala mseu waukulu wochoka ku Ejipito kupita ku Asiriya. Aasiriya adzayendera Aejipito, Aejipitonso adzayendera Aasiriya. Ndipo Aejipito ndi Aasiriya adzapembedza pamodzi. Tsiku limenelo Israele adzakhala pamodzi ndi Ejipito ndi Asiriya, ndipo maiko atatuwo adzakhala dalitso pa dziko lonse lapansi. Chauta Wamphamvuzonse adzaŵadalitsa ndi mau aŵa akuti, “Adalitsidwe Aejipito, anthu anga; adalitsidwe Aasiriya, ntchito ya manja anga; adalitsidwe Aisraele, osankhidwa anga.” Chaka china mtsogoleri wankhondo wotumidwa ndi Sarigoni, mfumu ya ku Asiriya, adaadzalimbana ndi mzinda wa Asidodi, naulanda. Nthaŵi imeneyo nkuti Chauta atalankhula kale kudzera mwa Yesaya mwana wa Amozi. Adaanena kuti, “Pita ukavule chiguduli m'chiwuno mwako ndi nsapato kuphazi kwako.” Ndipo iyeyo adaachitadi zimenezo. Ankangoyenda maliseche ndiponso opanda nsapato. Tsono mzinda wa Asidodi uja utalandidwa, Chauta adati, “Yesaya mtumiki wanga wakhala akuyenda maliseche ndiponso opanda nsapato zaka zitatu zapitazi. Chimenechi chakhala chizindikiro kwa Aejipito ndi Aetiopiya cholosera zimene zilikudza. Ndimo m'mene mfumu ya ku Asiriya idzachitire: idzatenga akapolo a ku Ejipito ndi opirikitsidwa ku Etiopiya, anyamata ndi okalamba, nidzaŵayendetsa ali maliseche ndi opanda nsapato, matako ao ali pamtunda. Zimenezi zidzachititsa manyazi Aejipitowo. Tsono onse amene ankadalira dziko la Etiopiya ndiponso amene ankakhulupirira Ejipito, adzamva chisoni ndi kuchita manyazi. Tsiku limenelo anthu okhala m'mphepete mwa nyanja adzati, ‘Onanitu zimene zachitikira anthu aja tinkaŵakhulupiriraŵa, amene tinkathaŵirako kuti atithandize ndi kutipulumutsa kwa mfumu ya ku Asiriya! Ha! Tsopano tonsefe tidzapulumuka bwanji?’ ” Nawu ulosi wonena za chipululu cha m'mbali mwa nyanja. Tsoka lidzafika kuchokera ku dziko lochititsa mantha monga m'mene kamvulumvulu amakunthira kuchokera ku chipululu. Ndaona zinthu zoopsa m'masomphenya: wofunkha akufunkha, woononga akuwononga. Ankhondo a ku Elamu, yambani nkhondo! Ankhondo a ku Mediya, zingani mzindawo. Ine Chauta ndidzathetsa mavuto onse amene adadza ndi Babiloni. Nchifukwa chake zimene ndidazimva ndi kuziwona m'masomphenya zija zandichititsa mantha, ndipo ndamva nazo ululu ngati mkazi amene akuchira. Ndikuvutika nazo zimene ndilikumva. Ndikuda nazo nkhaŵa zimene ndikuwonazi. Mtima wanga ukugunda, ndipo ndikunjenjemera ndi mantha. Ndakhala ndikulakalaka chisisira, koma chisisiracho chandibweretsera zoopsa. Iwo akukonza tebulo ndi kuyala mphasa, alikudya, alikumwa. Mwadzidzidzi alikumva mau akuti, Dzukani inu ankhondo, pakani mafuta zishango zanu! Pakuti Ambuye andiwuza kuti, “Pita, kaike mlonda kuti azinena zimene akuwona. Akamaona anthu aŵiriaŵiri okwera pa akavalo, okwera pa abulu ndi okwera pa ngamira, mlondayo akhale tcheru, tcherutu zedi!” Apo mlondayo adafuula kuti, “Ambuye, usana wonse ndimakhala pa nsanja, usiku wonse ndimakhala pa malo anga olondera. Ndidangoona kukubwera anthu okwera pa akavalo, akuyenda aŵiriaŵiri. Mmodzi mwa iwo adati, ‘Ii, wagwa, wagwatu uku Babiloni! Mafano onse a milungu yake aphwanyikira pansi.’ ” Ndiye abale anga Aisraele, inu opunthidwa ndi opetedwa ngati tirigu, tsopano ndakuuzani uthenga umene ndamva kwa Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele. Nawu ulosi wonena za Edomu: Wina akundilankhula mofuula kuchokera ku Edomu, akuti, “Iwe mlonda, usikuwu utha liti? Iwe mlonda, utha liti kodi usikuwu?” Mlonda akuti, “Kulikucha, koma kudanso. Ukafuna kufunsanso, ubwerenso udzafunse.” Nawu ulosi wonena za Arabiya: Inu anthu a ku Dedani oyenda pa gulu, amene usiku mumagona m'malunje a ku Arabiya, muŵapatse madzi anthu aludzu kuti amwe. Inu anthu a ku Tema, muŵapatse chakudya anthu othaŵa nkhondo. Pakuti akuthaŵa malupanga, malupanga osololasolola, mauta okokakoka, ndiponso nkhondo yoopsa. Ambuye adandiwuza kuti, “Chatsala chaka chimodzi, potsata m'mene amaŵerengera munthu waganyu, ndipo ulemu wonse wa anthu a ku Kedara udzatheratu. Mwa anthu onse amphamvu a ku Kedara okoka mauta, opulumuka adzakhala oŵerengeka.” Chauta, Mulungu wa Israele, watero. Nawu ulosi wonena za chigwa chooneramo zinthu m'masomphenya: Kodi chachitika nchiyani kuti nonse mukwere pa madenga? Ndinu anthu osokera, okhala mu mzinda wachiwawa ndi waphokoso. Anthu anu ophedwa sadaphedwe ndi lupanga, kapena kufera pankhondo. Atsogoleri anu onse adathaŵa nagwidwa, osaponyako ndi muvi umodzi womwe. Nonsenu amene mudapezeka mudagwidwa, ngakhale mudaathaŵiratu adani akali kutali. Nchifukwa chake ndidati, “Muchoke, mundileke ndilire ndi mtima woŵaŵa. Musayese kundipepesa pa za kuwonongeka kwa abale anga.” Nthaŵi ino ndi yamavuto, yogonjetsedwa ndiponso yachisokonezo m'chigwa chooneramo zinthu m'masomphenya. Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, ndiwo atichita zimenezi. Malinga adagumuka ndipo anthu adakalirira ku mapiri. Ankhondo a ku Elamu adadza atakwera pa akavalo, m'manja muli mauta ndi mivi, ndipo ankhondo a ku Kiri anali okonzeka ndi zishango zao. Zigwa zanu zachonde zinali zodzaza ndi magaleta, ndipo asilikali okwera pa akavalo adakaima kumaso kwa zipata za mzinda. Zonse zoteteza Yuda zidalandidwa. Tsiku limenelo mudayang'ana ku zida zankhondo zimene zinali m'Nyumba ya Nkhalango ija. Mudapeza malo ena m'makoma a mzinda wa Yerusalemu ali ogumuka. Mudasunga madzi m'chidziŵe chakunsi. Mudaŵerenga nyumba zonse mu mzinda wa Yerusalemu, ndipo mudagwetsa zina kuti mupeze miyala yokonzera makoma a mzindawo. Pakati pa makoma aŵiri mudamangapo chitsime chosungiramo madzi ochokera ku chidziŵe chakale. Koma simudaganizeko za Mulungu amene adachititsa zimenezi, simudasamaleko za Iye amene adazikonza kale lomwe. Nthaŵi imeneyo Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, adakuitanani kuti mulire ndi kudza misozi, kumeta ndi kuvala ziguduli. Koma inu mudakondwa ndi kusangalala, mudapha ng'ombe ndi nkhosa ndi kuzidya, ndiponso mudamwa vinyo. Mudati, “Tidye, timwe, poti maŵa tifa.” Chauta Wamphamvuzonse adandiwululira pondinong'oneza m'khutu kuti, “Ndithudi, tchimo limeneli sindidzakukhululukirani mpaka kufa kwanu,” akutero Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse. Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, adandiwuza kuti ndipite kwa Sebina, kapitao woyang'anira nyumba yaufumu, kukamufunsa kuti, “Kodi ukuchita chiyani kuno? Walimba mtima bwanji kuti udzikumbire manda kuno, kudzikumbira manda pa phiri, ndi kudzisemera mopumulira m'thanthwe? Chauta adzakugwira dzolimba ndi kukuponya mwamphamvu, iweyo wanyongawe. Adzakusandutsa ngati mpira ndipo adzakuponya m'dziko lalikulu. Kumeneko nkumene ukafere, ndipo magaleta ako amene unkanyadira adzatsalira komwekonso, iwe wochititsa manyazi nyumba ya mbuye wakowe. Chauta adzakuchotsa pa ukapitao wako, ndipo adzakutsitsa pakuthetsa udindo wako.” Chauta adauza Sebina kuti, “Tsiku limenelo ndidzaitana mtumiki wanga Eliyakimu, mwana wa Hilikiya. Ndidzam'veka mkanjo wako ndi lamba wako ndi kumpatsa ulamuliro wako. Tsono adzalamulira anthu onse okhala mu Yerusalemu ndiponso a fuko la Yuda. Ndidzampatsa makii a ulamuliro wa pa banja la mfumu Davide. Akadzatsekula, palibe amene adzatseke. Ndipo adzatseka, popanda wina wotsekula. Ndidzamulimbitsa ngati chikhomo pa udindo wakewo, ndipo adzakhala wopatsa ulemu kwa banja la atate ake. “Koma ana ndi adzukulu ake adzakhala katundu wolemera pa iye m'banja la atate ake, monga ngati ziŵiya zonse zimene zimapachikidwa pa chikhomo. Tsiku limenelo chikhomo chokhoma dzolimba chija chidzasukusa, chidzazuka ndipo chidzagwa. Tsono zonse zopachikidwa pachikhomopo zidzaonongedwa.” Akutero Chauta Wamphamvuzonse. Nawu ulosi wonena za Tiro. Fuulani mwachisoni, inu oyendetsa zombo za ku Tarisisi! Pakuti mzinda wa Tiro waonongeka, kulibenso nyumba kapena dooko! Zimenezi adazimva pochokera ku Kitimu. Khalani chete, inu anthu okhala m'mphepete mwa nyanja, inu amalonda a ku Sidoni! Amithenga anu adaoloka nyanja, ndipo adayenda pa nyanja zazikulu. Phindu lanu linali tirigu wa ku Sihore, zokolola za ku Nailo, ndipo munkachita malonda ndi anthu a mitundu yonse. Chita manyazi, iwe Sidoni, mzinda wamalinga wakunyanja, chifukwa nyanjayo yalankhula, yanena kuti, “Sindinamvepo zoŵaŵa za kubala, sindinaberekepo ana, ndipo sindinalerepo mwana, wamwamuna kapena wamkazi.” Aejipito adzadzidzimuka ndi kuchita mantha, akadzamva kuti Tiro adaonongeka. Thaŵirani ku Tarisisi, fuulani mwachisoni, inu okhala m'mphepete mwa nyanja. Kodi ndi uwu mzinda wa Tiro wotchukawu, mzinda wakalekale uja? Kodi ndi uwu mzinda uja unkatumiza anthu kuwoloka nyanja kukakhala ku maiko ena? Kodi ndani amene adakonza zimenezi kuti zigwere Tiro, mzinda uja wopereka ukulu kwa anthuwu, umene amalonda ake anali akalonga ndiponso otchuka kwambiri pa dziko lonse lapansi? Chauta Wamphamvuzonse ndiye adakonza zimenezi kuti athetse kunyada kwao, kuti atsitse anthu onse olemekezeka a pansi pano. Mubalalike m'dziko mwanu ngati mtsinje wa Nailo, inu anthu a ku Tarisisi. Palibenso china choti nkukutchinjirizani. Chauta watambalitsa dzanja lake kuloza nyanja ndipo wagwedeza maufumu. Walamula a ku Kanani kuti agwetse malinga ao. Ndipo adati, “Simudzakondwanso, inu anthu a mu mzinda wa Sidoni, mudzapanikizidwa, ndipo ngakhale muthaŵire ku Kitimu, nkumeneko komwe simukapeza mpumulo.” Onani dziko la Ababiloni, anthu ameneŵa palibenso, adatheratu. Aasiriya ndi amene asandutsa Tiro kuti akhale malo a zilombo. Adamanga nsanja zao zankhondo, adagumula malinga ake nasandutsa mzindawo bwinja. Lirani kwambiri, inu oyendetsa zombo a ku Tarisisi, chifukwa mzinda wanu wamalinga wagwetsedwa. Nthaŵi ikubwera pamene Tiro adzaiŵalika pa zaka makumi asanu ndi aŵiri, imene ili ngati nthaŵi ya moyo wonse wa mfumu imodzi. Zitatha zaka zimenezo, Tiro adzakhala ngati mkazi wachiwerewere uja woimbidwa nyimbo ija yakuti: “Tenga zeze wako, uzungulire mzinda, iwe mkazi wachiwerewere woiŵalika. Uimbe zezeyo mokometsera, uimbenso nyimbo zako zija, kuti anthu akukumbukire.” Zitatha zaka makumi asanu ndi aŵiri, Chauta adzachitapo kanthu pa Tiro. Mzindawo udzabwerera ku ganyu wake wakale uja. Ndipo adzachita zachiwerewere ndi maufumu a dziko lonse lapansi. Koma phindu lake ndi malipiro ake adzazipereka kwa Chauta. Sadzachita nazo kaligwiritsa kapena kuzikundika, koma adzazipereka kwa otumikira Chauta, kuti agule zakudya zambiri ndi zovala zokongola. Zoona, Chauta adzaononga dziko lapansi ndi kulisandutsa chipululu. Adzalisakaza, nadzamwaza anthu ake onse. Aliyense adzaona zimodzimodzi: ansembe ndi anthu, akapolo aamuna ndi ambuyao aamuna, adzakazi ndi ambuyao aakazi, ogula ndi ogulitsa, obwereka ndi oŵabwereka, ndiponso okongola ndi okongoza. Dziko lapansi lidzaonongedwa kwathunthu, lidzasakazikiratu, pakuti Chauta wanena zimenezi. Dziko likulira ndipo likufota. Dziko lonse lapansi likuvutika ndipo likuuma. Mlengalenga ukuvutika pamodzi ndi dziko lapansi. Anthu aipitsa dziko lapansi posatsata malamulo a Mulungu, ponyoza mau ake, ndipo pophwanya chipangano chamuyaya chimene Iye adapangana nawo. Nchifukwa chake Mulungu watemberera dziko lapansi, anthu am'dzikomo akuzunzika chifukwa cha machimo ao. Iwo amalizika, ndipo atsala ndi oŵerengeka okha. Mphesa zikuuma, ndipo vinyo akusoŵa. Aliyense amene ankasangalala ali ndi chisoni. Kulira kokometsera kwa ting'oma tao kwatha, phokoso la anthu osangalala latha, zeze wosangalatsa uja wati zii. Anthu saimbanso pomwa vinyo, akamamwa zaukali zimaŵaŵa m'kamwa mwao. Mu mzinda wachisokonezo uja zonse zaonongedwa, nyumba iliyonse yatsekedwa, kotero kuti palibe wotha kuloŵamo. Anthu akufuula m'miseu chifukwa cha kusoŵa kwa vinyo. Chimwemwe chonse chatheratu, palibenso chisangalalo pa dziko lonse lapansi. Mzinda wasanduka bwinja, zipata zake zagumuka. Zimenezi ndizo zimene zidzachitikire mtundu uli wonse wa pa dziko lapansi. Kudzakhala ngati khunkha la olivi ndi khunkha la mphesa, pamene kholola latha. Koma otsala aja adzafuula ndi kuimba mokondwa. Akuzambwe adzatamanda ukulu wa Chauta. Nchifukwa chake inu akuvuma, tamandani Chauta. Anthu okhala m'mphepete mwa nyanja, yamikani Ambuye, Mulungu wa Israele. Kuchokera ku maiko akutali tilikumva nyimbo zotamanda, zoyamika Wolungama uja. Koma ine ndikuti: Ndatheratu, ndatheratu! Tsoka kwa ine! Onyenga akupitirizabe ndipo kunyenga kwao kukupitabe m'tsogolo. Inu anthu a dziko lapansi, zoopsa, mbuna ndi misampha zikukudikirani. Aliyense wothaŵa phokoso la zoopsazo adzagwa m'mbuna, ndipo wotuluka m'mbunamo adzakodwa mumsampha. Kudzagwa mvula yachigumula ndipo maziko onse a dziko adzagwedezeka. Dziko lapansi lidzathyokathyoka, lidzang'ambika kwathunthu ndi kugwedezeka kwamphamvu. Dziko lapansi lidzadzandira ngati munthu woledzera, lidzagwedezeka ngati chisimba nthaŵi ya mkuntho. Dziko lapansi lalemedwa ndi zoipa zake, lidzagwa ndipo silidzaukanso. Tsiku limenelo Chauta adzalanga kumwamba zamphamvu zakumwamba, ndipo pansi pano mafumu a pansi pano. Mulungu adzasonkhanitsa mafumu onse pamodzi, ngati am'ndende amene ali m'dzenje. Adzaŵatsekera m'ndende, ndipo patapita nthaŵi yaitali, adzalangidwa. Mwezi udzanyala, ndipo dzuŵa lidzachita manyazi, pakuti Chauta Wamphamvuzonse adzakhala mfumu. Adzalamulira pa phiri la Ziyoni ndi ku Yerusalemu, ndipo adzaonetsa ulemerero wake pamaso pa akuluakulu. Inu Chauta, ndinu Mulungu wanga. Ndidzakulemekezani ndi kutamanda dzina lanu. Pakuti mwachita zinthu zodabwitsa mokhulupirika ndi motsimikiza, zinthu zimene mudakonzeratu kalekale. Mzinda uja mwausandutsa mulu wamiyala, Mzinda wamalinga uja mwausandutsa bwinja. Nyumba zamphamvu za adani athu si mzindanso tsopano, sizidzamangidwanso. Nchifukwa chake anthu amphamvu a mitundu yonse adzakutamandani, m'mizinda ya mitundu yankhalwe anthu adzakuwopani. Inu mwakhala ngati ngaka kwa anthu osauka, mwakhala ngati linga kwa anthu osoŵa pa nthaŵi yamavuto. Mwakhala ngati pobisalirapo namondwe, ndiponso ngati mthunzi wousirapo dzuŵa. Anthu ankhalwe ali ngati namondwe woomba pa khoma, ngati chitungu m'dziko louma. Inu mumaletsa phokoso la anthu achilendo. Monga momwe mthunzi wa mtambo umathetsera kutentha, momwemonso mumaletsa nyimbo ya anthu ankhalwe. Pa phiri ili la Ziyoni Chauta Wamphamvuzonse adzakonzera anthu a mitundu yonse phwando la zakudya zokoma ndi la vinyo wabwino, phwando la nyama yonona ndi la vinyo amene wafikapo. Pa phiri limeneli adzachotsa chisoni chimene chaphimba anthu a mitundu yonse, chimene chakuta mafuko onse. Chauta adzathetsa imfa mpaka muyaya, adzapukuta misozi m'maso mwa aliyense, ndipo adzachotsa manyazi a anthu ake pa dziko lonse lapansi. Watero Chauta. Tsiku limenelo aliyense adzati, “Uyu ndiye Mulungu wathu! Tidamkhulupirira kuti adzatipulumutsa. Iyeyu ndiye Chauta. Tidamkhulupirira, tsopano tiyeni tikondwe ndi kusangalala chifukwa choti watipulumutsadi.” Chauta adzateteza phirili ndi dzanja lake, ndipo Amowabu adzaŵapondereza pomwe aliripo, monga momwe manyowa amaŵaponderezera m'dzenje. Amowabuwo adzayesa kutambasula manja ao monga amachitira munthu wosambira. Koma Chauta adzathetsa kudzitama kwao ndiponso luso la manja ao. Adzagumula malinga ao ataliatali. Adzaŵagwetsa, kenaka adzaŵaponya pansi, pafumbi penipeni. Tsiku limenelo m'dziko la Yuda anthu adzaimba nyimbo iyi yakuti, “Tili ndi mzinda wamphamvu, Mulungu amautchinjiriza ndi zipupa ndi malinga. Tsekulani zipata za mzinda, kuti mtundu wotsata malamulo ndi wokhulupirika uloŵe. Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu. Inu anthu, mukhulupirire Chauta mpaka muyaya, chifukwa chakuti Chauta Mulungu ndiye thanthwe losatha. Iye watsitsa anthu okhala pa malo okwera, waononga mzinda wamphamvu uja. Wagumula zipupa zake, ndipo waugwetsera pansi, pafumbi penipeni. Mapazi a anthu akuupondereza, mapazi a anthu otsika, mapazi a anthu osauka.” Inu Chauta ndinu Wolungama, mumasalaza njira ya munthu womvera inu, Inu Chauta, ife timatsata njira ya malamulo anu, ndipo timakhulupirira Inu. Mtima wathu umangolakalaka kukumbukira ndi kulemekeza dzina lanu. Mtima wanga wonse umalakalaka Inu usiku, mzimu wanga m'kati mwa ine umakufunafunani. Pamene muweruza dziko lapansi, anthu onse okhalamo amaphunzira chilungamo. Munthu woipa mukamchitira zabwino, saphunzira zachilungamo. Amachita zoipa m'dziko lachilungamoli, ndipo amalephera kuzindikira ukulu wa Chauta. Inu Chauta, mwasamula dzanja lanu kuti muŵalange, koma iwo sakuliwona. Anthuwo achite manyazi poona m'mene mumakondera anthu anu, ndipo moto umene mwasonkhera adani anu, uŵapsereze. Inu Chauta, mumatipatsa mtendere, chifukwa choti zonse zimene timakhoza, mumatichitira ndinu. Chauta, Mulungu wathu, ife ngakhale takhala tikulamulidwa ndi ena, sitilemekeza dzina lina, koma lanu lokha. Ankhanza aja tsopano adafa, sadzakhalanso ndi moyo, sadzabweranso kudzativutitsa, pakuti mwaŵalanga ndi kuŵaonongeratu. Palibenso amene amaŵakumbukira. Koma Inu Chauta, mwachulukitsa mtundu wathu, mwaukulitsa ndithu. Mwakuza dziko lathu, mwalandirapo ulemu mbali zake zonse. Inu Chauta, pamene anali m'masautso, anthu anu adakufunafunani, pamene munkaŵalanga, adapemphera kwa Inu. Inu Chauta, mwatiliritsa monga momwe amalirira mkazi pa nthaŵi yobala mwana. Ife tidamva ululu, ndipo tidavutika ngati mkazi pa nthaŵi yobala mwana, koma sitidapindule kanthu. Sitidadzetse chipulumutso m'dziko lapansi pano, sitidabadwitse anthu atsopano pansi pano. Anthu anu amene adafa adzakhalanso ndi moyo, matupi ao adzauka. Inu nonse amene muli m'manda, dzukani ndi kuimba mosangalala. Monga momwe mame amafeŵetsera pansi kutsitsimutsa zomera, momwemonso Chauta adzaukitsa anthu amene adafa kale. Abale anga, pitani mukaloŵe m'nyumba zanu, ndipo mukadzitsekere. Mubisale pang'ono mpaka mkwiyo wa Chauta utatha. Chauta akubwera kuchokera kumene amakhala, akubwera kudzalanga anthu a dziko lapansi chifukwa cha machimo ao. Magazi okhetsedwa pa dziko lapansi adzaululuka, mitembo ya anthu ophedwa sidzabisikanso. Tsiku limenelo Chauta adzagwiritsa ntchito lupanga lake lakuthwa, lalikulu ndi lamphamvu, kulanga Leviyatani, chinjoka chothaŵa chija, Leviyatani njoka yozeŵezeka, ndipo adzaphanso chilombo choopsa cham'nyanja. Tsiku limenelo Chauta adzalankhula za munda wake wokoma wamphesa. Adzati, “Ine Chauta ndine mlonda wa mundawo, nthaŵi zonse ndimauthirira. Ndimaulonda usana ndi usiku, kuti wina angauwononge. “Sindidzaukwiyiranso munda wanga wamphesawo. Minga ndi mkandankhuku zidakati ziwoneke, ndikadalimbana nazo ndi kuzitentha kotheratu. Koma ngati adani a anthu anga afuna kuti ndiŵatchinjirize, apangane nane za mtendere, ndithu apangane nane za mtendere.” Masiku akudzawo, Yakobe adzazika mizu, Israele adzachita mphukira ndi maluŵa. Ndipo adzadzaza dziko lonse lapansi ndi zipatso zake. Kodi Chauta adalanga Aisraele monga m'mene adalangira adani ao? Kodi Aisraele adaphedwa monga m'mene adaphera adani ao? Chauta adaŵalanga pa kuŵapirikitsa ndi kuŵatumiza ku ukapolo. Adaŵachotsa ndi mpweya wake waukali, monga momwe kumachitikira pa tsiku la mkuntho wochokera kuvuma. Motero machimo a Israele adzakhululukidwa, ndipo adzaonetsa kulapa kwathunthu, akadzaphwanya miyala yonse ya maguwa achikunja ndi kuisandutsa fumbi. Maguwa ofukizapo lubani ndiponso mafano ofanizira Asera sadzaonekanso. Mzinda wamalinga wasanduka bwinja. Wasanduka malo osiyidwa ndi oiŵalika ngati chipululu. Kumeneko kwasanduka busa la ziŵeto, ndipo ziŵeto zimapumulako ndi kumadya nthambi za mitengo. Nthambi za mitengoyo zikauma, amazithyola, ndipo akazi amazitola nazisandutsa nkhuni. Popeza kuti anthuŵa ndi osamvetsa, nchifukwa chake Mulungu amene adaŵalanga sadzaŵamvera chisoni, Iye amene adaŵapanga sadzaŵachitira chifundo. Tsiku limenelo Chauta mwini wake adzasonkhanitsa anthu ake mmodzimmodzi, kuchokera ku mtsinje wa Yufurate mpaka ku mtsinje wa ku Ejipito. Tsiku limenelo lipenga lalikulu lidzalira kuitana Aisraele onse amene adaali mu ukapolo ku Asiriya ndi ku Ejipito. Iwowo adzabwera, ndipo adzapembedza Chauta pa phiri lake loyera la ku Yerusalemu. Tsoka kwa ufumu wonyada wa zidakwa za ku Efuremu! Tsoka kwa ulemerero wake umene wayamba kufota ngati duŵa, mzinda uja uli kumtunda kwa chigwa chachonde, umene amanyadira anthu oledzera vinyo. Ambuye ali naye wina wamphamvu ndi wanyonga. Iyeyo adzabwera ngati mkuntho wamatalala ndi namondwe woononga, ngati chigumula chamadzi chokokolola zonse, ndipo adzaŵagwetsa pansi mwankhanza. Kunyada kwa atsogoleri oledzera a ku Efuremu adzakuthetseratu kwenikweni. Ndipo ulemerero wa mzinda uja umene uli ngati duŵa lokhala kumtunda kwa chigwa chachonde wayamba kufota. Udzakhala ngati nkhuyu yoyambirira kupsa. Munthu akangoiwona, amaithyola ndi kuidya nthaŵi yomweyo. Tsiku limenelo Chauta Wamphamvuzonse adzakhala ngati chisoti chachifumu chaulemerero ndi nsangamutu yokongola kwa anthu ake otsala. Oweruza adzaŵapatsa mtima wachilungamo. Adzaŵalimbitsa mtima onse amene amalimbana ndi adani pa zipata za mzinda. Nawonso aŵa ali punzipunzi chifukwa cha vinyo, akudzandira ndi zakumwa zaukali. Ansembe ndi aneneri ali punzipunzi ndi zakumwa zaukali. Onsewo ndi osokonezeka chifukwa cha vinyo, ali dzandidzandi chifukwa cha zakumwa zaukali. Amamvetsa molakwa zimene amaziwona m'masomphenya, amalephera kuweruza milandu imene amadzaŵatulira. Pa matebulo onse pali masanzi okhaokha, palibenso malo opanda uve. Iwo akuti, “Kodi munthu ameneyu akuti aphunzitse yani? Kodi uthengawo akuti afotokozere yani? Kodi ndife ana ongoleka kumene kuyamwa, kapena makanda ongoŵachotsa kumene kubere? Akuyesa kumatiphunzitsa pang'onopang'ono lemba ndi lemba, mzere ndi mzere, phunziro ndi phunziro. Zonsezo akungoti apa pang'ono, apa pang'ono.” Ndithudi, Mulungu adzakuphunzitsani kudzera mwa anthu a chilankhulo chachilendo, anthu a chilankhulo chamtundu. Adaakuuzani kuti, “Malo opumulira ndi ano, otopa apumule, malo ousira ndi ano,” koma inu simudamvere. Nchifukwa chake Chauta adzakuphunzitsani pang'onopang'ono, lemba ndi lemba, mzere ndi mzere, phunziro ndi phunziro, kuti mudzakhumudwe poyenda. Mudzapweteka, mudzakodwa mu msampha, ndipo adzakutengani ku ukapolo. Tsopano mverani zimene Chauta akukuuzani, inu anthu achipongwe, amene mumalamulira anthu ake kuno ku Yerusalemu. Inu mumanena kuti “Ife tidachita chipangano ndi imfa, ndipo manda satiwopsa ai. Chiwonongeko chikamadzafika, sichidzatikhudza konse. Inu mumakhulupirira mabodza ngati kothaŵira, ndipo mumadalira kunama kuti kukhale kopulumukira.” Tsopano zimene akunena Ambuye Chauta nzakuti, “Ku Ziyoni ndikuika maziko a mwala wotsimikizika, mwala wapangodya wamtengowapatali wopanga maziko amphamvu. Pamwalapo palembedwa kuti, ‘Wokhulupirira sadzagwedezeka.’ Chilungamo ndicho chidzakhala ngati chingwe choyesera maziko ake, ndipo ungwiro udzakhala ngati choongolera chake. Koma matalala adzaononga mabodza amene mumaŵakhulupirira, ndipo chigumula chidzamiza malo anu opulumukirapo.” Chipangano chimene mudachita ndi imfa chidzatha, kotero kuti manda adzayamba kukuwopsani. Chiwonongeko chikamadzafika, chidzakugonjetsani. Nthaŵi iliyonse imene chizidzaoneka, chizidzakukanthani. Chizidzafika m'maŵa mulimonse, usana ndi usiku. Tsono anthu akadzamvetsa uthenga umenewu, adzaopsedwa kwambiri. Mudzakhala ngati munthu wogona pa bedi lalifupi kwambiri, kotero kuti sangatambalitsepo miyendo, ndiponso ngati munthu wofunda kabulangete kopereŵera. Chauta adzamenya nkhondo monga adachitira ku phiri la Perazimu. Adzakalipa monga adachitira ku chigwa cha Gibiyoni. Adzachita zimene afuna, ngakhale kuti zidzaoneke ngati zachilendo. Adzatsiriza ntchito yake, ntchito yake yozizwitsayo. Tsono inu musanyozere mau ameneŵa. Mukatero, maunyolo anu adzakuthinani koposa. Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, andiwuza kuti, “Ndagamula kuti ndidzaononga dziko lonse.” Tcherani khutu, ndipo mumve mau anga. Mvetserani ndipo mumve zimene ndikukuuzani. Kodi mlimi wofuna kubzala amangokhalira kutipula kokhakokha? Kodi amangokhalira kugaula ndi kugalauza? Akasalaza mundawo, suja amafesa maŵere ndi chitoŵe? Suja amafesa tirigu ndi barele m'mizere, nabzala mcheŵere m'mphepete mwa mundawo? Mulungu ndiye amamulangiza ndi kumphunzitsa njira yokhoza. Maŵere sapuntha poponderezapo ndi gareta lopanda mikombero, ndipo chitoŵe sapuntha popondetsapo mikombero ya gareta. Maŵere amapuntha ndi kamtengo, chitoŵe amaomba ndi ndodo. Tirigu sangamupunthe kosalekeza, kuwopa kuti angatekedzeke. Amampuntha poyendetsapo galeta, koma osatekedza njere zake. Nzeru zimenezi zimachokera kwa Chauta Wamphamvuzonse. Uphungu wake ndi wodabwitsa, nzeru zake nzopambana. Ariyele, Ariyele, tsoka kwa iwe, iwe mzinda umene Davide adamangako zithando zankhondo! Papite chaka chimodzi kapena ziŵiri, masiku onse achikondwerero apitirire ndithu, pamenepo Mulungu adzauthira nkhondo mzinda wa Ariyele. Tsono kudzakhala kulira ndi kudandaula, ndipo mzindawo udzasanduka ng'anjo ya guwa lansembe. Monga Davide, Mulungu adzamangako zithando zankhondo zolimbana ndi mzindawo, adzauzinga ndi nsanja zankhondo ndi kumanga mitumbira youthirira nkhondo. Tsono iwe Yerusalemu utagwetsedwa, udzalankhula uli pansi, mau ako adzamveka uli m'fumbi. Liwu lako lidzafumira pansi ngati la mzukwa, mau ako adzamveka ngati onong'ona kuchokera m'fumbi. Iwe Yerusalemu, chigulu cha adani ako chidzamwazika ngati fumbi, chigulu cha ankhondo ankhanza chidzabalalika ngati mungu wouluka. Ndipo mwadzidzidzi ndi mosayembekezeka, Chauta Wamphamvuzonse adzakupulumutsa ndi mabingu, zivomezi ndi phokoso lalikulu. Adzatumizanso kamvulumvulu, namondwe ndi malaŵi a moto woononga. Tsono chigulu cha mitundu ina yonse ya anthu othira nkhondo mzinda wa Ariyele, onse olimbana ndi mzindawo ndiponso linga lake lamphamvu ndi kuuzinga, onsewo adzazimirira ngati maloto, ngati zinthu zoziwona m'masomphenya usiku. Chigulu cha mitundu ina yonse ya anthu othira nkhondo Phiri la Ziyoni chidzakhala ngati munthu wanjala wolota kuti alikudya, koma podzuka, ali nayobe njala, kapena chidzakhalanso ngati munthu waludzu wolota kuti alikumwa, koma podzuka, kum'mero kudakali gwaa. Mudodome ndipo mukhale ozizwa. Dzichititseni khungu ndipo mukhalebe osapenya. Muledzere, koma osati ndi vinyo, ndipo mudzandire, koma osati ndi chakumwa chaukali. Chauta wakugonetsani tulo tofa nato. Wakutsekani maso, inu aneneri, wakuphimbani kumutu, inu olosa. Kwa inu zinthu zilizonse zoziwona m'masomphenya zakhala zobisika ngati mau a m'buku lomatirira. Buku limenelo atapatsa wina wodziŵa kuŵerenga kuti aŵerenge, iye adzati, “Sindingathe, chifukwa choti nlomatidwa.” Ngati bukulo mupatsa wina wosadziŵa kuŵerenga kuti aŵerenge, adzanena kuti “Sindidziŵa kuŵerenga.” Ambuye adati, “Anthu aŵa amati amapemphera kwa Ine, koma mau ao ndi opanda tanthauzo, ndipo mitima yao ili kutali ndi Ine. Chipembedzo chao ndi kungotsata chabe malamulo ongoŵaloŵeza pamtima, malamulo ochokera kwa anthu. Nchifukwa chake Ine ndidzapitiriza kuŵachitira zodabwitsa anthu amenewo. Nzeru za anthu ao anzeru zidzatha, ndipo kuchenjera kwa anthu ao ochenjera kudzazimirira.” Tsoka kwa amene amabisira Chauta maganizo ao, amene amachita ntchito zao mu mdima, namaganiza kuti palibe amene akuŵaona ndi kudziŵa zimene akuchita. Mwazondotsa zinthu zonse. Kodi chopambana nchiti, woumba kapena dothi loumbira? Kodi chinthu chopangidwa chingauze wochipanga kuti, “Sudandipange ndiwe?” Monga chingamuuze kuti, “Sukudziŵa chimene ukuchita?” Pajatu pakangopita kanthaŵi, nkhalango ya Lebanoni idzasanduka munda wachonde, ndipo munda wachonde udzasanduka nkhalango. Tsiku limenelo agonthi adzamva mau a m'buku, ndipo anthu akhungu amene ankakhala mumdima, adzapenya. Anthu odzichepetsa adzakhalanso ndi chimwemwe mwa Chauta, ndipo anthu osauka adzakondwa chifukwa cha Woyera uja wa Israele. Koma ankhanza adzatheratu, oseka anzao adzazimirira, ndipo opendekera ku zoipa adzaonongedwa. Mulungu adzalanga anthu osinjirira anzao, ndiponso ophophonyetsa anthu ozengedwa mlandu. Adzalanganso amene amapereka umboni wonama, kuti anzao osalakwa asaweruzidwe molungama. Motero tsono Chauta, Mulungu wa Israele, amene adapulumutsa Abrahamu pa mavuto, akunena kuti, “Anthu anga sadzanyozedwanso, nkhope zao sizidzagwanso ndi manyazi. Iwo, ndiye kuti ana ao, akadzaona zimene ndidachita Ine pakati pao, adzatamanda dzina langa loyera. Adzazindikira kuyera kwake kwa Woyera Uja wa Yakobe, ndipo adzachita naye mantha Mulungu wa Israele. Anthu opusa adzapeza nzeru, onyinyirika adzavomera malangizo.” Chauta akuti, “Tsoka kwa ana ondipandukira Ine! Amachita zodzikonzera okha osati zokonza Ine. Amachita chipangano chaochao, chosatsata chifuniro changa, ndipo amanka nachimwirachimwira. Amapita ku Ejipito kukapempha chithandizo, Ine osandifunsa. Amathaŵira kwa Farao kuti aŵatchinjirize, amakafuna malo opulumukirako ku Ejipito. Koma kutchinjiriza kwa Farao kudzakuchititsani manyazi, ndipo malo opulumukirako a ku Ejipitowo mudzachita nawo manyazi. Ngakhale kuti nduna zake zafika kale ku Zowani, ndipo akazembe ake afika kale ku Hanesi, anthu onse a ku Yuda adzamva manyazi chifukwa cha anthu opanda nawo phindu ndipo osaŵathandiza konse, koma ongobweretsa manyazi.” Nawu ulosi wonena za nyama za ku chipululu chakumwera: Akazembe akuyenda m'dziko loopsa m'mene muli mikango, mphiri ndi njoka zouluka. Amasenzetsa abulu ao mphatso zamtengowapatali ndipo chuma chao amasenzetsa ngamira zao, kupita kwa mtundu wa anthu umene sungaŵathandize. Chithandizo cha Ejipito nchachabe ndi chopanda phindu, choncho dzikolo ndalitcha dzina lakuti “Chilombo cholibwidika.” Mulungu adandiwuza kuti, “Tsopano pita, ukalembe zimenezi pa sileti iwo akuwona, ukazilembenso m'buku, kuti kutsogolo zidzakhale umboni wosatha. Ameneŵa ndi anthu opandukira Mulungu, ana onama, okana kumvera malangizo a Chauta. Amauza oona zobisika kuti, ‘Musaonenso.’ Amauza aneneri kuti, ‘Musatiloserenso zoona. Mutiwuze zotikomera, mutilosere zam'mutu chabe. Chokani apa, osakhala pa njira. Sitifuna kumvanso za Woyera uja wa Israele.’ ” Nchifukwa chake Woyera uja wa Israele akunena kuti, “Inu mumanyozera zimene ndimakuuzani, mumakhulupirira zopsinja anzanu ndipo mumadalira mabodza. Nchifukwa chake tchimo lanuli lidzakhala ngati mng'ankha pa chipupa chachitali choŵinuka, chimene kugwa kwake nkwadzidzidzi. Zidzakhala ngati kuphwanyika kwa mbiya, imene ili yotekedzekeratu, popanda ndi phale lomwe lopalira moto, kapena lotungira madzi m'chitsime.” Tsono Ambuye Chauta, Woyera uja wa Israele adati, “Ngati mutembenuka ndi kubwerera, mudzapulumuka. Ngati mudzinga ndi kukhulupirira, mudzakhala amphamvu.” Koma inu mudakana kutero. Mudati, “Tidzathamanga pa akavalo.” Chabwino, mudzathaŵe! Mudatinso, “Tidzakwera pa magareta aliŵiro.” Chabwino, koma okuthamangitsani adzakhalanso aliŵiro. Anthu chikwi chimodzi mwa inu adzathaŵa poona mdani mmodzi. Asilikali asanu okha adzakwanira kukuthamangitsani. Otsalira mwa inu adzakhala ngati mtengo wa mbendera wapaphiri, ngati chizindikiro chapagomo. Komabe Chauta akufunitsitsa kuti akukomereni mtima. Ali wokonzeka kuti akuchitireni chifundo, chifukwa Chauta ndi Mulungu wachilungamo. Ndi odala onse amene amakhulupirira Iye! Ndithudi, inu anthu a ku Ziyoni, okhala ku Yerusalemu, simudzaliranso. Mulungu adzakukomerani mtima pamene adzamva kulira kwanu, ndipo akadzangomva, pompo adzakuyankhani. Ngakhale Ambuye adzakuloŵetseni m'zovuta, adzakhala komweko kumakuphunzitsani, sadzabisala, mudzaŵaona. Pamene mupatukira kumanja kapena kumanzere, mudzamva kumbuyo kwanu mau okulozerani njira oti, “Njira ndi iyi, muyende m'menemu.” Pamenepo mudzatenga mafano anu, ena okutidwa ndi siliva, ena okutidwa ndi golide, ndipo mudzaŵataya ngati zinyalala, ndikunena kuti, “Zichoke zonsezi!” Mukamadzabzala mbeu zanu, Chauta adzakugwetserani mvula kuti zimere, ndipo mudzakolola zambiri. Tsiku limenelo ng'ombe zanu zidzapeza mabusa aakulu. Ng'ombe ndi abulu zokuthandizani kulima zidzadya chakudya chamchere chopapasa ndi fosholo ndi chifoloko. Pa tsiku limene nsanja zankhondo za adani anu zidzagwe, anthu ake naphedwa, pa phiri lililonse lalikulu ndi pa gomo lililonse lalitali, padzayenda mitsinje ya madzi. Mwezi udzaŵala ngati dzuŵa, ndipo dzuŵa lidzaŵala kwambiri ngati kasanunkaŵiri kuŵala kwa pa tsiku limodzi. Zimenezi zidzachitika pamene Chauta adzamange ndi kupoletsa zilonda zimene Iye yemwe adachititsa pakuŵalanga anthu ake. Onani, ulemerero wa Chauta ukuwonekera kuchokera kutali. Akuwonetsa mkwiyo m'kati mwa moto ndi m'kati mwa chiwutsi chatolotolo. Akulankhula mwaukali, ndipo mau ake akutentha ngati moto woononga. Mpweya wake uli ngati mtsinje wosefukira, wa madzi oyesa m'khosi. Akusefa anthu a mitundu ina ndi sefa wosakaza. Ngati akavalo, akuŵaika m'kamwa chitsulo choti chiŵasokeretse. Koma inu anthu a Mulungu, mudzakondwa ndi kuimba monga m'mene mumachitira usiku pa chikondwerero chopatulika. Mudzasangalala ngati anthu opita naimba toliro ku phiri la Chauta, thanthwe la Israele. Chauta adzamveketsa liwu lake loopsa, ndipo anthu adzaona dzanja lake likutsika pa iwo, ndi ukali woopsa ndi malaŵi a moto woononga, pakati pa mphezi, namondwe ndi matalala. Aasiriya adzaopsedwa ndi liwu la Chauta, pamene Iye adzaŵakantha ndi ndodo yake. Pamene Mulungu adzakhala akuŵalanga adani aja, anthu ake adzakhala akuvina ndi ting'oma ndi azeze. Mulungu mwini adzamenyana ndi Aasiriya. Malo otenthera zinthu ndi okonza kale, adakonzera mfumu ya ku Asiriya. Malowo ndi ozama ndi aakulu, odzaza ndi moto ndi nkhuni. Tsono mpweya wa Chauta, wonga ngati mtsinje wa sulufure, udzakoleza motowo. Tsoka kwa amene amapita ku Ejipito kukapempha chithandizo. Iwo amadalira akavalo, ndipo amakhulupirira kuchuluka kwa magaleta ao ankhondo, ndiponso mphamvu za asilikali ao okwera pa akavalo. Koma sakhulupirira Woyera uja wa Israele, kapena kupempha chithandizo kwa Chauta. Komabe Chautayo ndi wanzeru ndipo angathe kuwononga. Sabweza zimene wanena, adzalimbana ndi anthu oipa ndiponso ndi anthu amene amathandiza oipawo. Aejipito ndi anthu chabe, si milungu ai. Akavalo ao si mizimu, koma ndi nyama chabe. Chauta akachitapo kanthu, opereka chithandizo adzaphunthwa, olandira chithandizocho adzagwa, ndipo onsewo adzathera limodzi. Chauta adandiwuza kuti, “Monga momwe mkango kapena msona wa mkango umabangulira utagwira nyama, ndipo abusa sangaupirikitse, ngakhale auwopseze ndi kufuula chotani, motero palibe chimene chingaletse Chauta Wamphamvuzonse kutchinjiriza Phiri la Ziyoni ndi gomo lake. Monga mbalame zouluka pamwamba pa zisa zake, Chauta Wamphamvuzonse adzatchinjiriza mzinda wa Yerusalemu. Adzauteteza ndi kuupulumutsa, adzausiya pambali ndi kuuwombola.” Inu Aisraele, bwererani kwa Iye amene mudampandukira kwakukulu. Pajatu tsiku limenelo nonsenu mudzataya mafano anu asiliva ndi agolide, amene mudapanga ndi manja anu auchimo. “Aasiriya adzaonongedwa pa nkhondo, osati ndi mphamvu ya munthu. Adzaonongedwa ndi lupanga, lupanga lake osati la munthu. Adzathaŵa ku nkhondo, ndipo anyamata ao adzakhala akapolo. Mfumu yao idzathaŵa ndi mantha, ndipo atsogoleri ake ankhondo adzabalalika mwamantha kwambiri, kotero kuti adzasiya mbendera zao zankhondo,” akutero Chauta amene moto wake uli ku Ziyoni, ndipo ching'anjo chake chili ku Yerusalemu. Nthaŵi ina kudzakhala mfumu ina yolamulira mwaungwiro, ndiponso nduna zina zoweruza mwachilungamo. Aliyense mwa iwo adzakhala ngati pothaŵirapo mphepo ndi malo obisalirapo namondwe. Adzakhala ngati mitsinje yoyenda m'dziko louma, ndipo ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu m'chipululu. Maso a anthu openya sadzakhalanso otseka, ndipo makutu a anthu akumva adzakhala otchera. Anthu a mtima waphamphu adzadziŵa kuchita zinthu moganiza bwino, ndipo anthu achibwibwi adzalankhula mosadodoma ndi momveka. Chitsiru sichidzalandira ulemu, ndipo munthu woipa sadzalemekezeka. Munthu wopusa amalankhula zauchitsilu, ndipo amaganiza kuchita zoipa. Amachita zoipira Mulungu, amalankhula zonyoza Mulungu. Anjala saŵapatsa chakudya, aludzu saŵapatsa chakumwa. Munthu wachabechabe njira zake nzoipa. Amalingalira zaupandu kuti aŵachite chiwembu anthu osauka pakuŵanamizira, ngakhale pamene osaukawo ali osalakwa konse. Koma munthu wa mtima wabwino amalingalira zabwino, ndipo amalimbikira kuchita zabwino. Tatiyeni, inu akazi aulesi, mumve mau anga. Inu akazi odzitama, imvani zimene ndikulankhula. Pakapita chaka ndi masiku pang'ono, mudzanjenjemera inu akazi amatama, chifukwa mitengo ya mphesa idzakanika, zipatsonso sizidzaoneka. Dederani inu akazi aulesi, njenjemerani, inu odzikhulupirira udyo. Vulani zovala, ndipo muvale nsanza m'chiwuno. Dzimenyeni pa chifuŵa mwachisoni, chifukwa minda yachonde ndi yamphesa yaonongeka, ndipo minga ndi mkandankhuku zikumera pa dziko la anthu anga. Ndithu, mulire nyumba zonse zimene ankakhalamo mosangalala, ndiponso mzinda umene udaali ndi chimwemwe. Nyumba yaufumu idzasiyidwa, ndipo mzinda wonse udzakhala wopanda anthu. Malinga ake ndi nsanja yomwe zidzasanduka mapanga mpaka muyaya. Abulu akuthengo adzasangalala kumeneko, ndipo ziŵeto zidzapeza busa komweko. Koma Mulungu adzatitumizira mzimu wake, kuchokera kumwamba, ndipo dziko lachipululu lidzasanduka lachonde, minda yonse idzabereka dzinthu dzambiri. Pamenepo m'dziko lonse mudzakhala chilungamo, kuyambira ku chipululu mpaka ku minda yachonde. Chifukwa anthu onse akamachita zachilungamo, m'dziko mudzakhala mtendere ndi bata mpaka muyaya. Anthu a Mulungu adzakhala m'midzi yamtendere, m'nyumba zokhulupirika, ndiponso m'malo ousira abata. Komabe nkhalango idzaonongedwa ndi matalala, ndipo mzinda udzagwetsedwa mpaka pansi. Anthu adzakondwa kwambiri chifukwa adzakhala ndi madzi ambiri, ndipo abulu ndi ng'ombe zao azidzadya paliponse. Tsoka kwa iwe woonongawe, iwe amene sadakuwononge. Tsoka iwe wonyengawe, amene wina aliyense sadakunyenge. Iwe ukadzaleka kuwononga, adzakuwononga, ukadzaleka kunyenga, adzakunyenga. Mutichitire chifundo, Inu Chauta, tikukhulupirira Inu. Mutitchinjirize ndi dzanja lanu lamphamvu tsiku ndi tsiku, ndipo mutipulumutse pa nthaŵi yamavuto. Mukatulutsa liwu lanu longa bingu, mitundu ya anthu imathaŵa. Inu mukadzambatuka, mitundu ya anthu imabalalika. Amakundika zokunkha monga m'mene zimachitira ziwala. Anthu amalumphira zofunkhazo monga m'mene limachitira dzombe. Chauta ndi wolemekezeka kwambiri, pakuti akukhala pamwamba pa zonse. Adzadzaza mzinda wa Ziyoni ndi chilungamo ndi ungwiro. Adzakupatsani mtendere wokhazikika pa nthaŵi yanu. Adzakuninkhaninso chipulumutso chachikulu, luntha lambiri ndi nzerunso zambiri. Kuwopa Chauta ndiko kumapezetsa chuma chimenechi. Anthu ao olimba mtima akufuula m'miseu, akazembe odzayesa kudzetsa mtendere akulira kwamphamvu. M'miseu yaikuluikulu muli zii, palibe odzeramo. Zipangano zaphwanyidwa, mboni zanyozedwa, ndipo palibenso kulemekezana. Dziko likulira ndipo likunka lilikutha. Nkhalango za ku Lebanoni zafota, ndipo chigwa chachonde cha Saroni chasanduka chipululu. Mitengo ya ku dera la Basani ndi ya ku phiri la Karimele ikuyoyoka masamba. Chauta akunena kuti, “Tsopano ndichitapo kanthu, ndiwonetsa mphamvu zanga, ndipo ndidzakhala wolemekezeka kwambiri. Inu mumaganiza zachabechabe, ndipo zonse zimene mumachita nzopandapake. Zotuluka m'kamwa mwanu zili ngati moto umene udzakuwonongani inu nomwe. Anthu a mitundu ina adzakhala ngati miyala yotenthedwa popanga njereza, adzakhala ngati minga yodula, yotenthedwa pamoto. “Inu amene muli kutali, imvani zimene ndachita. Inu amene muli pafupi, dziŵani mphamvu zanga.” Mu mzinda wa Ziyoni anthu ochimwa agwidwa ndi mantha, anthu osasamala za Mulungu akunjenjemera. Akunena kuti, “Ndani mwa ife angathe kupirira m'moto woonongawo? Ndani mwa ife angathe kukhalamo m'moto wosatha?” Angathe kutero ndi amene amachita zolungama ndi kulankhula zoona, amene amakana phindu lolipeza monyenga, amene amakutumula manja ake kuti angagwire chiphuphu, amene amatseka makutu kuti angamve mau opangana za kupha anzao, amene amatsinzina kuti angaone zoipa. Munthu wotere adzakhala pa malo otetezedwa. Kothaŵirako iye kudzakhala ku malinga am'matanthwe. Chakudya azidzalandira, ndipo madzi sadzamsoŵa. Nthaŵi imeneyo mudzayang'ana mfumu yooneka mokongola, ndipo mudzaona dziko labwino lotambasukira kutali. Mumtima mwanu muzidzalingalira zimene zinkakuwopsani kale. Muzidzati, “Ali kuti wokhometsa msonkho uja?” Simudzaonanso anthu amwano aja amene chilankhulo chao nchosadziŵika, chachilendo ndi chosamveka. Onani Ziyoni, mzinda wa zokondwerera zathu zachipembedzo. Maso anu adzaona Yerusalemu, mzinda wamtendere, hema losasunthika. Zikhomo zake sizidzazuka, ndipo zingwe zake sizidzaduka. Kumeneko Chauta adzatiwonetsa ulemerero wake. Adzakhala malo a mitsinje yaikulu ndi yaing'ono. Ngalaŵa zankhafi sizidzapitapo, ndipo zombo zazikulu sizidzayendapo. Pakuti Chauta ndiye muweruzi wathu. Chauta ndiye wotilamula, Chauta ndiye mfumu yathu, ndiye amene adzatipulumutsa. Zingwe za zombo za adani athu zamasuka, sizingathe kulimbitsa mlongoti wake, ndipo matanga ake sangathe kufunyuluka. Tsono zofunkha zathu zidzakhala zochuluka kwambiri, kotero kuti pogaŵana, ndi opunduka omwe adzalandirako. Palibe ndi mmodzi yemwe m'dzikomo wodzanena kuti, “Ndikudwala,” ndipo anthu onse akumeneko machimo ao adzakhululukidwa. Inu anthu a mitundu yonse, bwerani pafupi kuti mumve, inu anthu onse tcherani makutu! Limvetsere dziko pamodzi ndi zonse zokhalamo, limvetsere dziko lapansi pamodzi ndi zonse zofuma m'menemo. Pakuti Chauta waŵakwiyira anthu a mitundu yonse, waŵapsera mtima magulu ao onse ankhondo, watsimikiza kuti adzaonongedwa, waŵapereka kuti aphedwe. Mitembo ya anthu ao ophedwa adzangoitaya kunja, nimaola ndi kumanunkha, ndipo mapiri adzafiira ndi magazi. Dzuŵa, mwezi ndi nyenyezi zidzanyenyeka, ndipo mlengalenga udzakulungika monga chimachitira chikopa. Nyenyezi zonse zidzayoyoka monga amachitira masamba a mpesa kapena a mkuyu. Chauta akuti, “Lupanga langa lakhutiratu kumwamba. Si ili likutsika kudzalanga Aedomu, anthu amene ndatsimikiza kuti ndiŵaononga.” Lupanga la Chauta lakhuta magazi, ndipo lakutidwa ndi mafuta. Magazi ake a anaankhosa ndi a mbuzi, ndipo mafuta ake a ku impso za nkhosa zamphongo. Pakuti Chauta ali ndi nsembe mu mzinda wa Bozira, ndiye kuti kuphedwa kwa anthu ambiri m'dziko la Edomu. Pamodzi ndi anthuwo zidzaphedwanso njati ndiponso ng'ombe zamphongo zazing'ono ndi zazikulu zomwe. Dziko lao lidzakhuta magazi, ndipo nthaka yao idzakutidwa ndi mafuta. Imeneyi ndiyo nthaŵi imene Chauta adzalipsira, pamene adzalanga adani a Ziyoni, ndi kuteteza anthu ake. Madzi a m'mitsinje ya ku Edomu adzasanduka phula, ndipo dothi lake lidzasanduka sulufure. Dziko lonse lidzasanduka phula lamoto. Motowo udzayaka usana ndi usiku, ndipo utsi udzafuka kosalekeza. Dziko lidzakhala chipululu pa mibadwo ndi mibadwo, palibe ndi mmodzi yemwe amene adzayendamonso. M'dzikomo muzidzakhala akabaŵi ndi nungu, akadzidzi ndi makwangwala. Chauta adzalisandutsanso dziko loguga ndi lopanda kanthu. Akuluakulu sadzasankhanso mfumu kumeneko, ndipo atsogoleri ake onse adzakhala atachotsedwa. Minga idzamera m'nyumba zake zankhondo zotetezedwa, khwisa ndi mitungwi zidzamera m'malinga mwake. Nkhandwe zizidzayendayenda m'menemo, nthiŵatiŵa zidzapezamo mokhala. Avumbwe adzakumana ndi afisi, nyama zakuthengo zizidzaitanizana. Kumeneko mizimu yoipa yausiku idzafika ndipo idzapeza malo opumulirako. Akadzidzi adzamangako zisa zao, nkuikirako mazira, ndi kuswa ana ao namaŵasamala. Adembo adzasonkhana kumeneko aŵiriaŵiri. Funafunani ndi kuŵerenga m'buku la Chauta. Mwa zolengedwazi palibe chimene chidzasoŵa, ndipo sipadzakhala nchimodzi chomwe chopanda chinzake. Pakuti Chauta walamula kuti zitero, ndipo mzimu wake wazisonkhanitsa pamodzi. Chauta ndiye wagaŵa dzikolo, wapatsa chilichonse chigawo chake. Dzikolo lidzakhala lao mpaka muyaya, ndipo zidzakhala m'menemo pa mibadwo yonse. Chipululu ndi dziko lopanda madzi zidzasangalala, dziko louma lidzakondwa ndi kuchita maluŵa. Dzikolo lidzakhala ndi maluŵa ochuluka ongodzimerera okha. Lidzasangalala ndi kufuula ndi chimwemwe. Lidzakhala ndi ulemerero wonga wa mapiri a ku Lebanoni, maonekedwe ake adzakhala okongola ngati a ku Karimele ndi Saroni. Aliyense adzaona ulemerero wa Chauta ndi ukulu wa Mulungu wathu. Mulimbitse manja ofooka, ndi kuŵapatsa mphamvu maondo olobodoka. Muuze onse a mtima wamantha kuti, “Limbani mtima, musachite mantha. Mulungu wanu akubwera kudzalipsira ndi kulanga adani anu. Akubwera kudzakupulumutsani.” Pamenepo maso a anthu akhungu adzaphenyuka, ndipo makutu a agonthi adzatsekuka. Opunduka adzalumpha ngati mphoyo, ndipo osalankhula adzaimba mokondwa. Akasupe adzatumphuka m'chipululu, ndipo mitsinje idzayenda m'dziko louma. Mchenga wotentha udzasanduka nyanja, ndipo dziko louma lidzasanduka la akasupe. Pamene panali mbuto za nkhandwe padzamera udzu ndi bango. Kumeneko kudzakhala mseu waukulu wotchedwa “Mseu Wopatulika.” Ochimwa sadzayendamo, ndipo zitsilu sizidzasokera m'menemo. Kumeneko sikudzakhala mikango, ndipo nyama zoopsa sizidzafikako, sizidzapezeka konse kumeneko. Koma okhawo amene Chauta adaŵapulumutsa, adzayenda mu mseu umenewu. Amene Chauta adaŵaombola adzabwerera, ndipo adzafika ku Ziyoni akuimba mosangalala. Kumeneko adzakondwa mpaka muyaya, ndipo adzaona chimwemwe ndi chisangalalo. Chisoni ndi kudandaula zidzatheratu. Chaka cha 14 cha ufumu wa Hezekiya, mfumu ya ku Yuda, Senakeribu mfumu ya ku Asiriya adathira nkhondo mizinda yonse yamalinga ya ku Yuda, nailanda. Pambuyo pake mfumu ya ku Asiriyayo idatuma kazembe wake wankhondo kuchokera ku Lakisi, kuti apite ndi gulu lalikulu lankhondo kwa Hezekiya ku Yerusalemu. Tsono kazembeyo adaima pafupi ndi ngalande yamadzi yochokera ku dziŵe lakumtunda, pa mseu waukulu wopita ku malo a mmisiri woyeretsa nsalu. Anthu atatu adatuluka mu mzinda nakakumana naye. Anthu ake ndi aŵa: mkulu woyang'anira nyumba ya mfumu, dzina lake Eliyakimu mwana wa Hilikiya, Sebina mlembi wa bwalo, ndi Yowa mwana wa Asafu, wolemba zochitika. Kazembe wankhondo uja adaŵauza kuti akanene kwa Hezekiya mau aŵa: “Mfumu yaikulu, mfumu ya ku Asiriya ikuti, ‘Chimene chikulimbitsa chikhulupiriro chako motere nchiyani? Kodi ukuganiza kuti mau okha nkulingana ndi luso ndi mphamvu pa nkhondo? Kodi tsono ukudalira yani kuti uzindigalukira? Makamaka ukuyembekeza kuti Ejipito adzakuthandiza. Koma kuteroko kuli ngati kukhulupirira bango lothyoka limene litha kum'baya munthu m'manja ataliyesa ndodo yoyendera. Ndimo m'mene mfumu ya ku Ejipito imamchitira aliyense woidalira. “Kapena undiwuza kuti mumakhulupirira Chauta Mulungu wanu.” Kodi si Mulungu yemweyo amene akachisi ake ndi maguwa ake, Hezekiya adaŵathetsa, nauza anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti, “Muzipembedza pa guwa ili la ku Yerusalemu?” Tiye tsono utembezane ndi mbuye wanga, mfumu ya ku Asiriya: Ndidzakupatsa akavalo okwanira zikwi ziŵiri ngati iwe ungathe kupeza anthu ake okwerapo. Ungathe bwanji kupambana ngakhale mmodzi yekha mwa akazembe ang'onoang'ono a mbuye wanga, pamene ukukhulupirira Aejipito, kuti akupatse magaleta ndi anthu okwera pa akavalo? Ndiponso kodi sukudziŵa kuti ndi Chauta amene wandibweretsa kuno, ndidzathire nkhondo dziko lino ndi kuliwononga? Chautayo ndiye adachita kundiwuza kuti ndilimbane nalo ndi kuliwononga dziko lino.’ ” Pamenepo Eliyakimu, Sebina ndi Yowa adauza kazembeyo kuti, “Pepani, mutilankhule m'Chiaramu atumiki anufe, poti timachimvetsa. Musatilankhule m'Chiyuda, pakuti anthu onse ali pakhomaŵa alikumva.” Koma kazembe uja adati, “Kodi mukuganiza kuti mfumu yanga idandituma kuti ndilankhule mau ameneŵa kwa inu nokha ndi kwa mfumu yanu basi? Iyai, ndikulankhulanso kwa anthu amene akhala pakhomowo, amene adzayenera kudya ndoŵe yao yomwe ndi kumwa mkodzo wao womwe, monga momwe mudzachitire inuyo.” Tsono kazembe uja adaimirira nafuula m'Chiyuda kuti, “Mverani mau a mfumu yaikulu, mfumu ya ku Asiriya. Mfumuyo ikuti, ‘Musalole kuti Hezekiya akunyengeni, chifukwa sadzatha kukupulumutsani. Asakukakamizeni kuti mudalire Chauta pokuuzani kuti mosapeneka konse Chauta wanuyo adzakupulumutsani, ndipo kuti mfumu ya ku Asiriya sidzalanda mzinda wanuwu. Musamumvere Hezekiya. Mfumu ya ku Asiriya ikukulamulani kuti mutulukemo mumzindamo, ndipo muigonjere. Mukatero, aliyense mwa inu azidzadya mphesa ndi nkhuyu zake ndi kumamwa madzi a m'chitsime chake, mpaka nthaŵi imene mfumuyo idzakutengeni kupita nanu ku dziko lolingana ndi lanuli, dziko la mwana alirenji. Ndiye inu chenjerani, Hezekiya asakupusitseni pokuuzani kuti Chauta adzakupulumutsani. Mwa milungu ya anthu a mitundu ina, kodi alipo ndi mmodzi yemwe amene adapulumutsapo dziko lake kwa mfumu ya ku Asiriya? Kodi milungu ya Hamati ndi Aripadi ili kuti tsopano? Nanga milungu ya Sefaravaimu ili kuti? Kodi milunguyo idaupulumutsa mzinda wa Samariya kwa mbuye wanga? Kodi ndi iti mwa milungu ya maikoŵa imene idapulumutsapo maiko ake kwa mfumu yathu, kuti inu muziti Chauta nkupulumutsa Yerusalemu kwa mfumu yathuyo?’ ” Koma anthu adangokhala chete osayankhapo kanthu, chifukwa mfumu Hezekiya adaaŵalamula kuti, “Musamuyankhe ai.” Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya amene ankayang'anira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo, ndi Yowa mwana wa Asafu, wolemba zochitika, adang'amba zovala zao mwachisoni, ndipo adapita kwa mfumu Hezekiya nakamuuza zimene kazembe wa ku Asiriya uja adaalankhula. Hezekiya atangomva zimenezi, adang'amba zovala zake mwachisoni, ndipo adavala chiguduli, nakaloŵa m'Nyumba ya Chauta. Tsono adatuma Eliyakimu mkulu wa nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa mfumu, ndiponso ansembe akuluakulu, onse atavala ziguduli, kuti apite kwa mneneri Yesaya, mwana wa Amozi. Iwowo adauza Yesaya mau a Hezekiya onena kuti, “Lero ndi tsiku la mavuto, la chilango ndi la manyazi. Tili ngati mkazi wapathupi amene ali pafupi kubala mwana, koma alibe mphamvu zomubalira mwanayo. Mfumu ya ku Asiriya yatuma kazembe wake wankhondo kudzanyoza Mulungu wamoyo. Makamaka Chauta, Mulungu wanu, wamva kunyoza kumeneku, ndipo adzaŵalanga anthu amene adamunyozawo. Motero muŵapempherere anthu otsalaŵa amene akali ndi moyo.” Pamene Yesaya adamva mau a mfumu Hezekiyawo, adati, “Kauzeni mbuyanu mau a Chauta akuti, ‘Usade nawo nkhaŵa mau ondinyoza a atumiki a mfumu ya ku Asiriya. Ndidzaika mumtima mwa mfumuyo ganizo lina lakuti, ikadzangomva mphekesera, idzaumirizidwa kubwerera ku dziko lake, ndipo Ine ndidzamphetsa kwao komweko.’ ” Kazembe wankhondo uja adamva kuti mfumu ya ku Asiriya ija inachoka ku Lakisi, ndipo inali kuchita nkhondo ndi mzinda wa Libina. Motero anapita kumeneko kukakambirana nayo. Tsono pamene mfumu ya ku Asiriya idamva kuti mfumu Tirihaka wa ku Etiopiya akubwera kudzachita nayo nkhondo, idatumanso amithenga kwa mfumu Hezekiya ndi mau onena kuti, “Mulungu wako amene ukumkhulupirirayo asakunyenge pokulonjeza kuti Yerusalemu sadzagwa m'manja mwa ine mfumu ya ku Asiriya. Wakhala ulikumva zimene mafumu a ku Asiriya adaŵachita maiko onse, kuti adaŵaononga kotheratu. Tsono iweyo ndiye nkupulumuka? Makolo anga adaononga mizinda ya Gozani, Harani ndi Rezefe. Ndipo adapha anthu a ku Edeni amene ankakhala ku Telasara. Kodi milungu ya anthu a mitundu inawo idaŵapulumutsa? Nanga mafumu a m'mizinda ya Hamati, Aripadi, Sefaravaimu, Hena ndi Iva, ali kuti?” Mfumu Hezekiya adalandira kalata kwa amithenga aja, naiŵerenga. Pomwepo adapita ku Nyumba ya Chauta, naika kalatayo m'menemo pamaso pa Chauta, ndipo adapemphera kuti, “Inu Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, amene mumakhala pa mpando wanu waufumu pamwamba pa akerubi, inu nokha ndinu Mulungu wolamulira maufumu onse a dziko lonse lapansi. Mudalenga dziko lakumwamba ndi dziko lapansi. Tsono Inu Chauta, tcherani khutu, mumve. Inu Chauta tsekulani maso, muwone. Mumve mau onse amene Senakeribu adalankhula, onyoza Inu Mulungu wamoyo. Inu Chauta, zoonadi mafumu a ku Asiriya adaononga anthu a mitundu ina yonse, nasandutsa maiko ao chipululu. Adatentha milungu yao imene siinali milungu konse, koma mafano amitengo ndi amiyala opangidwa ndi anthu, nchifukwa chake adaiwononga. Ndiye Inu Chauta, Mulungu wathu, mutipulumutse ife kwa munthu ameneyu, kuti mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadziŵe kuti Inu nokha, Chauta, ndiye Mulungu.” Tsono Yesaya, mwana wa Amozi, adatumiza kwa mfumu Hezekiya mau ochokera kwa Chauta, Mulungu wa Israele, oyankha pemphero lake lija lonena za Senakeribu, mfumu ya ku Asiriya. Poitsutsa za mfumuyo Chauta adati, “Mzinda wa Ziyoni ukukunyoza ndi kukuseka, iwe Senakeribu, mzinda wa Yerusalemu ukupukusa mutu kumbuyo kwako monyodola. “Kodi iwe wanyoza ndi kulalatira yani? Kodi ndani amene wamufuulira ndi kumuyang'ana monyada? Si wina ai, koma Woyera uja wa Israele! Udatuma atumiki ako kudzanyoza Ine, ndipo udati, ‘Ndi magaleta anga ochuluka ndidakwera mapiri ataliatali, ndidafika mpaka pa nsonga za mapiri a ku Lebanoni. Ndidagwetsa mitengo yake ya mkungudza yaitali kwambiri, ndiponso mitengo yake ya paini yabwino koposa. Ndidaloŵanso m'kati mwake mwenimweni, mwankhalango yake yoŵirira kwabasi. Ndidakumba zitsime ku maiko achilendo ndi kumwamo madzi. Ndi mapazi anga ndidapondereza ndi kuumitsa mitsinje ya ku Ejipito.’ “Koma Ine Chauta ndikuti, Kodi sudamvepo kuti zimenezi ndidazikonzeratu kalekale? Ndidaaziganiziratu masiku amakedzana. Tsopano ndazichitadi. Iweyo kwako kunali kungogwetsa mizinda yamalinga ndi kuisandutsa miyulu ya miyala. Anthu amene ankakhala kumeneko anali opanda mphamvu, ankada nkhaŵa, ndipo adaasokonezeka. Anali ngati mbeu zam'munda, ngati udzu wanthete. Anali ngati udzu wapadenga, umene mphepo imauumitsa usanakule nkomwe. “Koma Ine ndimadziŵa zonse za iwe pamene ukukhala pansi, pamene ukuyenda kwina ndi kubwerako, ndiponso pamene ukundikwiyira. Chifukwa chakuti udandikwiyira, ndipo kudzitukumula kwako kudamveka kwa Ine, ndidzakola mphuno yako ndi mbedza, ndi kuika chitsulo m'kamwa mwako. Ndidzakubweza pokuyendetsa m'njira yomwe udadzera pobwera.” Tsono Yesaya adauza mfumu Hezekiya kuti, “Chizindikiro cha zimene zidzachitika ndi ichi: Chaka chino mudzadya tirigu wa mphulumukwa. Chaka chamaŵa mudzadya tirigu wongodzimerera. Tsono chaka chamkucha mudzabzala tirigu ndi kukolola, mudzaoka mitengo yamphesa nkudya zipatso zake. Anthu a m'banja la Yuda amene adzatsalire, adzapezanso bwino, ngati zomera zimene zazimitsa mizu pansi ndi kubala zipatso poyera. Ku Yerusalemu kudzafumira anthu otsala, ku phiri la Ziyoni kudzachokera gulu la anthu opulumuka. Changu cha Chauta Mphambe chidzachitadi zimenezi. “Zimene akunena Chauta za mfumu ya ku Asiriya, ndiizi, akuti, ‘Sadzaloŵa mu mzinda umenewu, sadzaponyamo muvi ndi umodzi womwe. Ankhondo ake azishango sadzafika pafupi ndi mzinda umenewu, ndipo sadzauzinga ndi mtumbira wankhondo. Adzabwerera potsata njira yomwe adaadzera pobwera, ndipo sadzaloŵa mu mzinda umenewu. Ine Chauta ndatero. Ine ndidzautchinjiriza ndi kuuteteza mzinda umenewu chifukwa cha ulemerero wanga, ndiponso chifukwa cha chipangano changa chimene ndidachita ndi Davide mtumiki wanga.’ ” Mngelo wa Chauta adapita ku zithando zankhondo za Aasiriya, naphako asilikali 185,000. M'maŵa mwake anthu adangoona asilikaliwo ali ngundangunda, atafa onsewo. Tsono Senakeribu, mfumu ya ku Asiriya, adachoka ndi kubwerera kwao, nakakhala ku Ninive. Tsiku lina pamene ankapembedza m'nyumba ya Nisiroki, mulungu wake, ana ake aŵiri, Adrameleki ndi Sarezere, adamupha ndi malupanga ao, nathaŵira ku dziko la Ararati. Ndipo Esarahadoni, mwana wake wina, adaloŵa ufumu m'malo mwake. Nthaŵi imeneyo mfumu Hezekiya adaadwala, ndipo anali pafupi kufa. Mneneri Yesaya, mwana wa Amozi, adapita kukamuwona, namuuza kuti, “Chauta akuti ukonze zonse bwino lomwe, poti ufa, suchira ai.” Pomwepo Hezekiya adatembenuka nayang'ana ku khoma, nayamba kupemphera kwa Chauta kuti, “Inu Chauta, mukumbukire kuti ndakhala ndikukutumikirani mokhulupirika ndi modzipereka. Ndipo nthaŵi zonse ndinali kuchita zokukomerani.” Atatero adayamba kulira ndi mtima woŵaŵa. Tsono Chauta adalamula Yesaya kuti, “Pitanso kwa Hezekiya, ukamuuze kuti, ‘Ine Chauta, Mulungu wa kholo lako Davide, ndamva pemphero lako, ndipo misozi yako ndaiwona. Nchifukwa chake ndidzakuwonjezera zaka khumi ndi zisanu pa moyo wako. Ndidzakupulumutsa iwe pamodzi ndi mzindawu kwa mfumu ya ku Asiriya, ndipo mzindawu ndidzautchinjiriza.’ ” Yesaya adauza Hezekiya kuti, “Chauta adzakupatsani chizindikiro kutsimikiza kuti adzasunga lonjezo lake. Akuti, ‘Chithunzithunzi chimene dzuŵa likuchititsa pa makwerero a Ahazi, ndidzachibweza m'mbuyo makwerero khumi.’ ” Ndipo chithunzithunzicho chidabwereradi m'mbuyo makwerero khumi. Ndakatulo ya Hezekiya mfumu ya ku Yuda, amene adaadwala kenaka nkuchira: “Ndinkaganiza kuti ndizipita ku dziko la akufa, ndidakali mnyamata wabiriŵiri, ndipo kuti ndidzakhala komweko mpakampaka. Ndinkaganiza kuti pa dziko lino la anthu amoyo, sindidzaonanso Chauta, anthu okhala pansi pano sindidzaŵapenyanso. Moyo wanga walandidwa ndi kuchotsedwa, ngati hema logwetsedwa, ngati nsalu yodulidwa ku makina ake oombera. Kuyambira m'maŵa mpaka usiku mwakhala mukunditsiriza. Usiku wonse mpaka m'maŵa ndinkalira ndi ululu. Munkaphwanya mafupa anga onse, monga umachitira mkango. Kuyambira m'maŵa mpaka usiku mwakhala mukunditsiriza. “Ndinkalira ngati namzeze wovutika, ndinkabuula ngati nkhunda yodandaula. Maso anga adaatopa nkuyang'ana kumwamba. Inu Ambuye, ndili m'mavuto, dzanditetezeni. Kodi ndinganene chiyani? Chauta walankhula nane, ndipo wachita zimenezi ndiye amene. Pa moyo wanga wonse ndidzakhala wovutika, chifukwa cha kuŵaŵa kwa mtima wanga. “Inu Ambuye, anthu amakhala moyo ndi zimenezi, moyo wa mzimu wanga uli mu zomwezo. Mundichiritse ndi kundibwezera moyo. Chimene ndidamvera zoŵaŵa nkuti ndipeze bwino. Mwapulumutsa moyo wanga ku manda, mwataya machimo anga onse kumbuyo kwanu. Akumanda sangathe kukuyamikani, akufa sangathe kukutamandani. Otsikira ku manda sangathe kukukhulupirirani. Amoyo, amoyo okha, ndiwo amakutamandani, monga m'mene ndikuchitira ine tsopanomu. Atate amauza ana ao za kukhulupirika kwanu. “Chauta wandipulumutsa, ndipo tidzamtamanda poimba ndi azeze m'Nyumba mwa Chauta pa moyo wathu wonse.” Pamenepo Yesaya adati, “Anthu atenge ntchintchi yankhuyu, aimate pa chithupsa, ndipo mfumu Hezekiya adzachira.” Tsono mfumu Hezekiya adafunsa kuti, “Kodi chizindikiro chake nchiyani chotsimikizira kuti ndidzapita ku Nyumba ya Chauta?” Nthaŵi imeneyo Merodaki-Baladani, mwana wa Baladani, mfumu ya ku Babiloni, adatuma amithenga naŵapatsira makalata ndi mphatso kuti akapereke kwa Hezekiya, poti adaamva kuti ankadwala ndipo adachira. Hezekiya adaŵalandira anthuwo, naŵaonetsa nyumba yosungiramo zinthu zake, monga siliva, golide, zokometsera chakudya, mafuta onunkhira amtengowapatali, zida zonse zankhondo ndiponso zonse zimene ankazisunga m'nyumba zake zosungiramo chuma. Panalibe kanthu kalikonse m'nyumbamo ndi mu ufumu wake wonse kamene sadaŵaonetse. Tsono mneneri Yesaya adapita kwa mfumu Hezekiya namufunsa kuti, “Kodi anthu amene aja adakuuzani zotani, ndipo adaachokera kuti?” Hezekiya adayankha kuti, “Adaachokera ku dziko lakutali, ku Babiloni.” Yesaya adamufunsanso kuti, “Kodi m'nyumba mwanumo adaona chiyani?” Hezekiya adayankha kuti, “Adaona za m'nyumba mwanga. Palibe ndi chimodzi chomwe chimene sindidaŵaonetse m'nyumba zanga zosungiramo chuma.” Pamenepo Yesaya adauza Hezekiya kuti, “Chauta Mphambe akunena kuti nthaŵi idzafika pamene zonse za m'nyumba mwanu ndi zonse zimene makolo anu adazisonkhanitsa mpaka lero lino, adzakulandani kupita nazo ku Babiloni. Sipadzatsalapo ndi kanthu kamodzi komwe. Ena mwa ana anu, obereka inu nomwe, adzatengedwa, ndipo adzaŵasandutsa adindo ofulidwa kuti azikatumikira ku nyumba ya mfumu ku Babiloni.” Tsono mfumu Hezekiya adauza Yesaya kuti “mau amene Chauta walankhulaŵa ndi abwino.” Ponena zimenezo, ankaganiza kuti, “Palibe kanthu ai, malinga kuti padzakhale mtendere ndi bata masiku onse a moyo wanga.” “Atonthozeni mtima, atonthozeni mtima anthu anga,” akutero Mulungu wanu. “Muŵalankhule mofatsa anthu a ku Yerusalemu. Muŵauze kuti nthaŵi ya mavuto ao yatha, machimo ao akhululukidwa. Ndaŵalanga moŵirikiza chifukwa cha machimo ao.” Kukumveka mau akuti, “Konzani njira ya Chauta m'thengo, lungamitsani mseu wa Mulungu wathu m'chipululu. Chigwa chilichonse achidzaze, phiri lililonse ndi gomo lililonse alitsitse. Dziko lokumbikakumbika alisalaze, malo azitundazitunda aŵasandutse zidikha. Motero ulemerero wa Chauta udzaoneka, anthu onse adzauwona. Chauta mwini wake ndiye wanena zimenezi.” Kudamveka mau akuti, “Lengeza.” Ine ndidafunsa kuti, “Kodi ndilengeze chiyani?” Mau aja adati, “Ulengeze kuti anthu onse ali ngati udzu. Kukongola kwao kuli ngati maluŵa akuthengo. Udzu umauma, maluŵa amafota, Chauta akaziwuzira mpweya wake. Ndithudi anthu sasiyana ndi udzu. Udzu umauma, maluŵa amafota, koma mau a Mulungu wathu adzakhalapo mpaka muyaya.” Kwera pa phiri lalitali, iwe wokalengeza uthenga wabwino ku Yerusalemu. Ufuule kwamphamvu, iwe wokalengeza uthenga wabwino ku Ziyoni. Kweza mau, usaope. Uuze mizinda ya ku Yuda kuti, “Mulungu wanu akubwera.” Zoonadi, Ambuye Chauta akubwera kudzaweruza mwamphamvu, ndipo akulamulira ndi dzanja lake. Akubwera ndi malipiro ake, watsogoza mphotho yake. Adzasamala nkhosa zake ngati mbusa. Adzasonkhanitsa anaankhosa ndi kuŵakumbatira. Ndipo adzatsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa. Kodi ndani adayesa kuchuluka kwa madzi am'nyanja ndi chikhatho chake, kapena kuyesa kutalika kwa mlengalenga ndi dzanja lake? Ndani adayesa dothi lonse la dziko lapansi ndi dengu? Ndani adayesa kulemera kwa mapiri ndi magomo pa sikelo? Ndani adalamulirapo maganizo a Chauta? Ndani adamphunzitsapo kanthu ngati mlangizi wake? Kodi Chauta adapemphapo nzeru kwa yani, kuti adziŵe zinthu? Ndani adamuphunzitsa kuweruza molungama? Ndani adamphunzitsa kudziŵa zinthu? Ndani adamlangiza njira ya kumvetsa zinthu? Mitundu ya anthu ili ngati kadontho ka madzi mu mtsuko, ilinso ngati fumbi chabe pa sikelo. M'manja mwa Chauta zilumba nzopepuka ngati fumbi. Nkhalango ya ku Lebanoni siingakwanitse nkhuni zosonkhera moto, nyama zam'menemo sizingakwanire kuperekera nsembe yootcha. Mitundu yonse ya anthu si kanthu konse pamaso pa Chauta, Iye amaziyesa zachabe ndi zopandapake. Kodi Mulungu mungathe kumuyerekeza ndi yani? Kodi mungamufanizire ndi chiyani? Likakhala fano, ndi munthu waluso amene amalipanga, kenaka mmisiri wa golide amalikuta ndi golide, nalipangira ukufu wasiliva. Mmphaŵi wosatha kupeza choperekera nsembe, amasankhula mtengo umene sudzaola. Amafunafuna mmisiri woti ampangire fano limene silingagwedezeke. Monga simudadziŵe? Monga simudamve? Kodi poyamba ponse sadakuuzeni? Kodi simudamvetse za kakhazikitsidwe ka dziko lapansi? Dziko lapansi lidalengedwa ndi Iye amene amakhala pa mpando wake waufumu kumwamba, kuseri kwa mlengalenga. Amaona anthu pansi ngati ziwala. Adafunyulula mlengalenga ngati nsalu yotchingira, ngati hema lokhalamo anthu. Amatsitsa mafumu amphamvu, olamulira dziko amaŵasandutsa achabechabe. Iwo ali ngati mbeu zobzala posachedwa, kapena zofesa chatsopano, zongoyamba kumene kuzika mizu. Mbeuzo Chauta akaombetsa mphepo zimauma, ndipo mkuntho umaziwulutsa ngati mankhusu. Woyera Uja akuti, “Kodi mungathe kundiyerekeza ndi yani? Kodi alipo wina wolingana nane?” Yang'anani kumlengalenga. Kodi ndani adalenga nyenyezi mukuziwonazi? Ndiye amene amazitsogolera ngati gulu lankhondo, ndipo iliyonse amaiitana ndi dzina lake. Popeza kuti nyonga ndi mphamvu zake nzazikulu. Palibe ndi imodzi yomwe imene imasoŵapo. Iwe Yakobe, ukulankhuliranji? Iwe, Israele, ukuneneranji kuti Chauta sakudziŵa za mavuto ako, kapenanso kuti sakusamalapo za iwe? Kodi sudziŵa? Kodi sudamve? Chauta ndiye Mulungu wachikhalire, Mlengi wa dziko lonse lapansi. Satopa kapena kufooka, palibe amene amadziŵa maganizo ake. Amalimbitsa ofooka, ndipo otopa amaŵaonjezera mphamvu. Ngakhale achinyamata amalefuka ndi kufooka, ngakhale anyamata amaphunthwa ndi kugwa. Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse. Mulungu akuti, “Mukhale chete ndipo mundimvere, inu maiko a m'mphepete mwa nyanja. Anthu a mitundu yonse akhale ndi mphamvu zatsopano. Asendere ndi kulankhulapo. Tiyeni tikhale pamodzi pa mlandu atiweruze. “Kodi ndani adabweretsa wogonjetsa uja wochokera kuvuma, wonka napambana kulikonse kumene amapita? Ndani amamthandiza kuti apambane anthu a mitundu ina, ndi kugonjetsa mafumu? Lupanga lake limaŵasandutsa anthuwo kukhala ngati fumbi lapansi, uta wake umaŵamwaza ngati mankhusu. Amaŵalondola namayenda mosavutika, m'njira zimene mapazi ake sadayendemo kale. Ndani adachita zimenezi mpaka kuzitsiriza, osakhala amene adayambitsa mitundu yonse ya anthu? Ndi Ineyo, Chauta, amene ndine chiyambi, ndipo ndidzakhalabe yemweyo pakati pa otsiriza.” Anthu a maiko a m'mphepete mwa nyanja aona zimene ndachita ndipo aopsedwa, anthu a pa mathero a dziko lapansi ali njenjenje. Akusendera pafupi, akubwera. Aliyense akuthandiza mnzake, akuuza mbale wake kuti, “Limba mtima.” Mmisiri wa matabwa amalimbikitsa mmisiri wosungunula golide, wosalaza fano ndi nyundo amalimbikitsa wolisanja pa chipala, ndipo ponena za kuwotcherera amati, “Kwachitika bwino.” Kenaka amalikhomerera fanolo ndi misomali kuti lisagwedezeke. Koma iwe Israele mtumiki wanga, iweyo Yakobe amene ndakusankhula, ndiwe mdzukulu wa Abrahamu bwenzi langa. Ndidakutenga kuchokera ku mapeto a dziko lapansi, ndidakuitana kuchokera ku mbali zakutali za dziko. Ndipo ndidzakuuza kuti, “Iwe ndiwe mtumiki wanga, ndidakusankhula, sindidakutaye.” Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa. Motero onse amene akukupsera mtima adzachita manyazi ndi kunyazitsidwa. Amene akumenyana nawe adzakhala ngati salinso kanthu, ndipo adzafa. Udzafunafuna amene amakangana nawe, koma osaŵapeza. Amene amamenyana nawe nkhondo adzakhala ngati salinso kanthu. Ine, Chauta Mulungu wako, ndikukugwira dzanja, ndine amene ndikukuuza kuti, “Usachite mantha, ndidzakuthandiza.” Usaope, iwe Yakobe, wofooka ngati nyongolotsi, usachite mantha, iwe Israele, wooneka ngati mtembo, chifukwa Ineyo ndidzakuthandiza. Mpulumutsi wako ndine, Woyera uja wa Israele. Ndidzakusandutsa ngati chipangizo chopunthira tirigu, chatsopano, cha mano akuthwa. Udzanyenya mapiri ndi kuŵaphwanyaphwanya. Magomo udzaŵasandutsa mankhusu. Udzaŵapeta, ndipo adzauluka ndi mphepo nadzamwazika ndi namondwe. Koma iwe udzakondwa chifukwa choti Ine ndine Mulungu wako. Udzapeza ulemerero chifukwa cha Ine, Woyera uja wa Israele. Pamene amphaŵi ndi osauka akufunafuna madzi, koma osaŵapeza, ndipo kum'mero kwao kwangoti gwa ndi ludzu, Ine Chauta ndidzayankha pemphero lao, Ine Mulungu wa Israele sindidzaŵasiya. Ndidzayendetsa mitsinje pakati pa zitunda zouma, ndipo akasupe adzatumphuka m'zigwa. Ndidzasandutsa chipululu kukhala chidziŵe cha madzi, ndi dziko louma kukhala akasupe. M'chipululu ndidzameretsa mkungudza, kasiya, mchisu ndi mtengo wa olivi. M'dziko louma ndidzabzala mitengo ya paini ya mitundu itatu. Choncho anthu adzaona ndi kudziŵa, adzazindikira ndi kumvetsa kuti Chauta ndiye adachita zimenezi, kuti Woyera uja wa Israele ndiye adakonza zimenezi. Chauta akuuza milungu kuti, “Dzafotokozeni mlandu wanu.” Chauta, Mfumu ya Yakobe akuti, “Perekani umboni wanu. Mubwere kuno, mudzatiwuze zam'tsogolo. Mufotokozere bwalo zamakedzana, kuti tiziganizire, ndipo tidziŵe zotsatira zake, kapena mutiwuze zakutsogolo. Tiwuzenitu zimene zidzachitike kutsogolo kuti tidziŵe kuti ndinu milungudi. Chitani zabwino kapena kubweretsa masoka, kuti mutidabwitse ndi kutichititsa mantha. Inuyo sindinu kanthu konse, ndipo zochita zanu nzopandapake. Amene amakupembedzaniyo amandinyansa. “Ndautsa munthu wina kumpoto, ndipo wabwera. Munthuyo, kuchokera chakuvuma, amamva kuitana pomutchula dzina. Amaponda olamulira ngati matope, monga m'mene munthu woumba mbiya amapondera mtapo. Ndani adaululiratu zimenezi poyamba pomwe kuti ife tidziŵe? Ndani adatiwuziratu zimenezi zisanachitike, kuti ife tinene kuti, ‘Wakhoza?’ Palibe ndi mmodzi yemwe adazinena, palibe ndi mmodzi yemwe adazilengeza, ndipo palibe amene adamva mau anu. Ine Chauta ndine amene ndidayambirira kumuuza Ziyoni kuti, ‘Si awo! Akubwera!’ Ndine amene ndidatuma munthu wokanena uthenga wabwinowu ku Yerusalemu. Koma ndikayang'ana, palibe ndi mmodzi yemwe: palibe wotha kulangiza, palibe wotha kuyankha mafunso anga. Ndithudi, milungu yonseyi njachabe, zochita zake si kanthu konse. Mafano ake osungunula ali ngati mphepo yachabechabe.” Chauta akuti, “Nayu mtumiki wanga amene ndimamchirikiza, amene ndamsankhula, amene ndimakondwera naye. Ndaika Mzimu wanga mwa iyeyo, ndipo adzaweruza anthu a mitundu yonse mwachilungamo. Sadzafuula kapena kukweza mau, mau ake sadzamveka mu mseu. Bango lopindika sadzalithyola, moto wozilala sadzauzima. Adzabweretsa chilungamo mokhulupirika. Sadzafookera kapena kutaya mtima, mpaka atakhazikitsa chilungamocho pa dziko lapansi. Maiko akutali akuyembekeza malamulo ake.” Mulungu, Chauta, adalenga zakuthambo ndi kuziyalika. Adalenga dziko lapansi ndi zonse zimene limabereka. Adapatsa mpweya kwa anthu okhala m'dzikomo, ndi kuninkha moyo kwa onse oyendamo. Iyeyo akunena kuti, “Ine Chauta ndakuitana kuti ukhazikitse chilungamo. Ndakugwira padzanja ndi kukusunga. Ndakusankhula kuti ukhale chipangano kwa anthu, ukhale kuŵala kounikira anthu a mitundu ina. Udzaŵatsekula maso anthu akhungu, udzamasula akaidi m'ndende, udzatulutsa m'ndende anthu okhala mu mdima. Ine ndine Chauta, dzina langa nlimenelo. Ulemerero wanga sindidzapatsa wina aliyense. Mayamiko oyenera Ine, sindidzalola kuti mafano alandireko. Zinthu zimene ndidalosa zija zachitikadi. Tsono ndikuuzani zinthu zatsopano, zisanaoneke ndikukudziŵitsiranitu.” Imbirani Chauta nyimbo yatsopano. Mtamandeni, inu okhala m'dziko lonse lapansi! Mtamandeni, inu zolengedwa zonse zam'nyanja. Imbani, inu maiko akutali ndi onse okhala kumeneko. Chipululu ndi mizinda yake zitamande Mulungu. Midzi ya Akedara imuyamike. Okhala mu mzinda wa Sela amuimbire mokondwa, afuule pa nsonga za mapiri. Atamande Chauta, ndipo alalike ulemu wake ku maiko akutali. Chauta akupita ku nkhondo ngati ngwazi, akuutsa ukali wake ngati munthu wankhondo. Akukuŵa, akufuula mfuu zankhondo. Akuwonetsa mphamvu zake pakuposa adani ake. Mulungu akuti, “Ndakhala ndili chete pa nthaŵi yaitali, ndidangoti phee, osachita kanthu. Koma tsopano ndikubuula ngati mkazi pa nthaŵi yake yochira, ndikupuma modukiza ndipo ndili ŵefuŵefu. Ndidzaononga mapiri ndi magomo, ndidzaumitsa udzu ndi mitengo yonse kumeneko. Ndidzasandutsa mitsinje kuti ikhale zilumba, ndipo ndidzaumitsa maiŵe. Ndidzatsogolera anthu akhungu m'miseu imene sadaidziŵe, ndidzaŵaperekeza pa njira zimene sadadzerepo konse. Ndidzasandutsa mdima wa kutsogolo kwao kuti ukhale kuŵala, ndipo ndidzasalaza malo osasalala. Zimenezi ndidzazichitadi ndipo sindidzazilekera padera. Onse amene akhulupirira mafano, amene amatchula mafanowo kuti, ‘Ndinu milungu yathu,’ adzatsitsidwa, ndidzaŵachititsa manyazi kotheratu.” Chauta akuti, “Mverani, agonthi inu! Muyang'ane ndipo mupenye, akhungu inu! Kodi ndani ali wakhungu osakhala mtumiki wanga? Ndani ali gonthi ngati wamthenga amene ndikumtuma? Kodi ndani ali wakhungu ngati wokhulupirika wanga? Ndani ali gonthi ngati mtumiki wa Chauta? Iwe waona zambiri, koma zonsezo sudazisamale. Makutu ako ndi otsekuka, koma suumva.” Chifukwa cha chilungamo chake, Chauta adafunitsitsa kuti malamulo ake akhale opambana ndi aulemu. Koma tsono anthu ameneŵa aŵalanda ndi kuŵafunkhira zinthu zao. Onseŵa adaŵakola m'mbuna, ndi kuŵabisa m'ndende. Adaŵafunkhira, popanda wina woŵapulumutsa, adaŵabera, popanda wina wonena kuti, “Bwezani!” Kodi alipo wina mwa inu amene adzamvetsere zimenezi? Ndani adzatchere khutu ndi kuzisamala kutsogolo kuno? Ndani adapereka Yakobe kwa ofunkha? Ndani adapereka Israele kwa anthu akuba? Kodi akuchita zimenezi si Chauta? Paja tidamchimwira, sitidatsate njira zake, ndipo sitidamvere malamulo ake. Motero adatikwiyira kwambiri, nativutitsa ndi nkhondo. Adayatsa moto ponseponse potizungulira, ife osamvetsa. Moto udatipsereza, koma ife osapezapo phunziro ai. Koma tsopano Chauta amene adakulenga iwe Yakobe, amene adakuumba iwe Israele, akunena kuti, “Usaope, chifukwa ndidakuwombola, ndidachita kukutchula dzina lako, ndiwe wanga. Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha. Pajatu Ine ndine Chauta, Mulungu wako. Ndine Woyera uja wa Israele, Mpulumutsi wako. Ndidzapereka Ejipito pofuna kuwombola iwe. Ndidzapereka Etiopiya ndi Seba m'malo mwa iwe. Popeza kuti ndiwe wanga wapamtima, ndidzapereka anthu m'malo mwa iwe. Chifukwa ndiwe wamtengowapatali pamaso panga, ndipo ndimakukonda, ndidzapereka mitundu ya anthu pofuna kuwombola moyo wako. Usaope, ndili nawe. Ndidzabweza zidzukulu zako kuchokera kuvuma, ndidzakusonkhanitsani nonse kuchokera kuzambwe. Ndidzauza akumpoto kuti ‘Muŵaleke.’ Ndidzalamula akumwera kuti ‘Musaŵagwire.’ Ana anga aamuna abwerere kuchokera ku maiko akutali, ana anga aakazi abwerere kuchokera ku mathero a dziko lapansi. Onsewo amadziŵika ndi dzina langa, ndidaŵalenga chifukwa cha ulemerero wanga, ndidaŵapanga ndi kuŵapatsa moyo.” Mulungu akunena kuti, “Itanani anthu anga ku bwalo la milandu. Maso ali nawo, koma sakupenya. Makutu ali nawo, koma sakumva. Mitundu yonse ya anthu isonkhane, anthu a m'maiko onse akhalepo pamlandupo. Ndani mwa iwo adaathapo kuneneratu zimenezi? Ndani mwa iwo adaathapo kutifotokozera zakale? Abwere ndi mboni zao, kuti zidzatsimikize mau ao, kuti anthu ena amve ndi kunena kuti, ‘Nzoonadi.’ Inu Aisraele, ndinu mboni zanga, ndinu atumiki anga amene ndidakusankhulani, kuti mundidziŵe ndi kundikhulupirira, ndipo mumvetse kuti Mulungu ndine ndekha. Patsogolo panga sipadapangidwepo mulungu wina, ndipo pambuyo panga sipadzakhalanso wina. Chauta ndi Ineyo, mpulumutsi wanu ndine ndekha. Ndine amene ndidaneneratu zimenezi, ndipo ndine ndidakupulumutsani. Si mulungu wina wachilendo amene adazichita pakati pa inu. Inu nomwe ndinu mboni zanga, ndikutero Ine Chauta. Ine ndine Mulungu ndipo ndidzakhalapo nthaŵi zonse. Palibe amene angathe kuthaŵa m'manja mwanga, palibe amene angathe kusintha zochita zanga.” Chauta, Momboli wanu, Woyera uja wa Israele, akunena kuti, “Ndidzatuma gulu lankhondo kukalimbana ndi Babiloni, kuti ndikupulumutseni. Ndidzagwetsa zipata za mzindawo, ndipo kukondwa kwa anthu ake kudzasanduka kulira. Ine ndine Chauta, Woyera wanu uja, Mlengi wa Israele. Ine ndekha ndine mfumu yanu.” Kale lija Chauta adapanga njira pa nyanja, njira pakati pa madzi amphamvu. Adasonkhanitsa magaleta ndi akavalo, ndiponso gulu lankhondo ndi asirikali amphamvu. Onsewo adagwa osadzukanso, adazimitsidwa ndi kutheratu ngati chingwe cha nyale. Iyeyo akunena kuti, “Musakumbukire zakale kapena kumaganiziranso zinthu zimene zidachitika kale. Ndikuchita zinthu zatsopano. Zayamba kale kuwoneka, kodi simukuzipenya? Ndikulambula mseu m'chipululu, ndipo ndikukupatsani mitsinje m'dziko louma. Nyama zakuthengo zidzandilemekeza, nkhandwe ndi nthiŵatiŵa zidzanditamanda, chifukwa ndidzayendetsa madzi m'chipululu ndipo ndidzayendetsa mitsinje m'dziko louma, kuti ndiŵapatse madzi anthu anga osankhidwa. Amenewo ndi anthu amene ndidadzilengera, ndipo azindiimbira nyimbo zotamanda Ine.” Chauta akuti, “Koma simudapemphere kwa Ine, inu am'banja la Yakobe, mudatopa nane, inu Aisraele. Simudadzatule kwa Ine nkhosa kuti zikhale zopereka zopsereza, simudandilemekeze ndi nsembe zanu. Sindidakulemetseni pomakupemphani zopereka zanu, sindidakutopetseni pomakupemphani lubani. Simudandigulire bango lonunkhira, simudandipatse mafuta okwanira a nsembe zanu. Koma m'malo mwake inu mwanditopetsa ndi machimo anu, mwandilemetsa ndi zolakwa zanu. “Ine, Ineyo ndithu, ndine amene ndimafafaniza machimo anu, kuti ulemerero wanga uwoneke. Sindidzasungabe mlandu wa machimo anu. Mundikumbutse zakale, titsutsane. Mufotokoze mlandu wanu kuwonetsa kuti simudalakwe. Atate anu oyamba adachimwa, atsogoleri anu aja adandilakwira. Mafumu anu adaipitsa malo anga opatulika. Nchifukwa chake ndidalola kuti banja la Yakobe liwonongedwe, ndidalola kuti Aisraele anyozedwe.” Chauta akunena kuti, “Mverani tsopano, inu am'banja la Yakobe. Inu Aisraele, ndinu atumiki anga, osankhidwa anga. Ine ndine Chauta amene ndidakulengani ndi kukuumbani m'mimba mwa amai anu, amenenso ndinkakuthandizani. Usaope iwe Yakobe, mtumiki wanga. Inu ndinu anthu anga okondedwa amene ndidakusankhulani. Ndidzathira madzi pa dziko louma, ndidzayendetsa mitsinje m'chipululu. Ndidzatumizira ana anu Mzimu wanga, ndidzatsitsa madalitso anga pa zidzukulu zanu. Iwo adzakula bwino ngati udzu wothirira bwino, ngati misondodzi yomera m'mbali mwa mitsinje. Wina adzanena kuti ‘Ine ndine wa Chauta,’ wina adzadzitchula wa m'banja la Yakobe. Winanso adzalemba padzanja pake kuti, ‘Wa Chauta,’ ndipo adzadzitchula wa m'banja la Israele.” Chauta, Mfumu ndi Momboli wa Israele, Chauta Mphambe, akunena kuti, “Ine ndine woyamba ndi womaliza. Palibenso Mulungu wina, koma Ine ndekha. Ndani nanga akulingana ndi Ine? Aimirire, alankhule, andifotokozere. Kuyambira kalekale ndani adalosa zakutsogolo? Atidziŵitsetu zimene zikudzachitika. Musadedere, musaope. Suja kuyambira kale lomwe ndakhala ndikukuuzani ndi kutsimikiza zimenezi? Inuyo ndinu mboni zanga. Kodi aliponso Mulungu wina kupatula Ine? Iyai, palibenso Thanthwe lina, sindikudziŵa lina lililonse.” Onse amene amapanga mafano ngachabe, milungu imene amailemekeza kwambiri ndi yopanda phindu. Amene amaipembedza ndi akhungu ndi osadziŵa kanthu, choncho adzaŵachititsa manyazi. Phindu lake nchiyani kupanga kamulungu kapena kusungunula fano lachabechabe? Onse opembedza fanolo adzaŵachititsa manyazi. Opanga mafano ndi anthu chabe. Onse asonkhane, aonekere ku bwalo la milandu. Onsewo adzaopsedwa, ndipo adzachita manyazi. Mmisiri wa zitsulo amatenga chitsulo nachiika pa moto. Ndi dzanja lake lamphamvu amachisula pakuchimenya ndi nyundo. Pambuyo pake amamva njala natha mphamvu, akapanda kumwa madzi, amalefuka. Mmisiri wa matabwa amayesa mtengo ndi chingwe. Amalembapo chithunzi ndi cholembera, nachizokota ndi zipangizo zake. Amachipanga ngati munthu, munthu wake wokongola, kuti achiike m'nyumba ya chipembedzo. Amagwetsa mitengo ya mkungudza. Mwinanso amasankhula mtengo wa paini kapena wa thundu ku nkhalango. Mwina mwake amabzala mtundu wina wa paini ndipo umakula ndi mvula. Mtengowo munthu amachitako nkhuni. Nthambi zina amasonkhera moto wootha, zina moto wophikapo buledi. Chigawo china cha mtengowo amapangira kamulungu nayamba kukapembedza. Amapanga fano namaligwadira. Chigawo china amasonkhera moto wootchapo nyama imene amadya mpaka kukhuta. Amaothanso motowo namanena kuti, “Aha! Ndikumva kufunda! Ati kukoma motowu ati!” Ndi chigawo chotsala amapanga kamulungu kake, fano lake limenelo. Amaliŵeramira ndi kumalipembedza. Amapemphera kwa fanolo namanena kuti, “Iwe ndiwe mulungu wanga, undipulumutse.” Anthu otere sadziŵa kanthu ndipo samvetsa konse. Maso ao ndi omatirira, sangathe kupenya. Nzeru zaonso nzogontha, sangathe kumvetsa. Palibe wolingalira, palibe wanzeru kapena womvetsa woti anganene kuti, “Chigawo china cha mtengo ndidatentha pa moto, pa makala ake ndidaphikapo buledi, ndidaotchapo nyama ndipo ndidadya. Tsopano chigawo chotsalachi ndipangira chinthu chonyansa! Monga ine ndizipembedza mtengo?” Munthuyo akuchita ngati kudya phulusa, maganizo ake opusa amsokeretsa kotero kuti sangapulumutsenso moyo wake. Sangathenso kudzifunsa kuti, “Kodi chinthu chili m'manja mwangachi si chabodza?” Chauta akunena kuti, “Ukumbukire zimenezi, iwe Yakobe, popeza kuti ndiwe mtumiki wanga, iwe Israele. Ndidakulenga, ndiwe mtumiki wanga. Iwe Israele sindidzakuiwala. Ndachotsa zolakwa zako ngati mtambo ndiponso machimo ako ngati nkhungu. Bwerera kwa Ine poti ndakuwombola.” Imbani mokondwa, inu zolengedwa zamumlengalenga, pakuti Chauta wagwiradi ntchito. Fuula iwe dziko lapansi. Yambani nyimbo, inu mapiri, ndiponso inu nkhalango ndi mitengo yanu yonse, chifukwa Chauta waombola Yakobe, waonetsa ulemerero wake mwa Israele. Chauta, Mpulumutsi wako, amene adakupanga m'mimba mwa mai wako, akunena kuti, “Ndine Chauta, amene ndidapanga zinthu zonse. Pamene ndinkayalika zakuthambo, ndinali ndekha. Pamene ndinkalenga dziko lapansi, kodi analipo amene adandithandiza? Ndine amene ndimalepheretsa mipingu ya anthu onama, ndi kupusitsa anthu oombeza ula. Ndine amene ndimatsutsa mau a anthu anzeru, ndi kuŵaonetsa kuti nzeru zao nzopusa. Ndine amene ndimatsimikiza mau a mtumiki wanga, ndi kupherezetsa zimene amithenga anga adaneneratu. Ndine amene ndimanena za Yerusalemu kuti anthu adzakhalanso kumeneko, ndi kunenanso za mizinda ya ku Yuda kuti idzamangidwanso. Ine ndidzautsanso malo ao amene adagwetsedwa. Ndine amene ndimauza nyanja yaikulu kuti, ‘Uma, ndipo mitsinje yakonso ndiiwumitsa.’ Ndine amene ndimanena za Kirusi kuti ‘Iye uja ndi mbusa wanga, adzachita zonse zimene ndikulinga! Adzalamula kuti Yerusalemu amangidwenso, ndipo kuti maziko a Nyumba ya Mulungu aikidwe.’ ” Chauta akulankhula ndi wodzozedwa wake Kirusi amene adamgwira dzanja lamanja, kuti agonjetse mitundu ina ya anthu, aŵathe mphamvu mafumu, ndi kutsekula zitseko kuti zipata zisatsekeke. Akunena kuti, “Ndidzayenda patsogolo pako, ndi kusalaza zitunda. Ndidzaphwanyaphwanya zitseko zamkuŵa, ndipo ndidzathyolathyola mipiringidzo yake yachitsulo. Ndidzakupatsa chuma chosaoneka poyera ndi katundu wa m'malo obisika. Motero udzadziŵa kuti ndine Chauta, Mulungu wa Israele, amene ndikukuitana pokutchula dzina. Chifukwa cha mtumiki wanga Yakobe, chifukwa cha wosankhidwa wanga Israele, ndikukuitana potchula dzina lako, ndikukupatsa dzina laulemu ngakhale iwe sukundidziŵa. Chauta ndine, palibenso wina, kupatula ine palibe Mulungu wina. Ndidzakupatsa mphamvu ngakhale sukundidziŵa. Ndidzachita zimenezi kuti kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe aliyense adziŵe kuti palibe wina koma Ine ndekha. Chauta ndine, palibenso wina. “Ndimalenga kuŵala ndi mdima, ndimadzetsa madalitso ndi tsoka. Ndine, Chauta, amene ndimachita zonsezi. “Gwetsa mvula, iwe thambo, kuchokera kumwamba, mitambo ikhuthule chilungamo chopulumutsa. Dziko lapansi litsekuke kuti patuluke chipulumutso, kuti chilungamo chimerepo. Ndine, Chauta, amene ndidalenga zimenezi.” Tsoka kwa amene amakangana ndi mlengi wake, ngakhale ali ngati phale chabe pakati pa mapale anzake. Kodi mtapo ungafunse munthu woumba kuti, “Kodi ukuumba chiyani?” Kapena kunena kuti, “Woumbawe, ulibe luso!” Tsoka kwa wofunsa bambo wake kuti, “Mwabereka chiyani,” kapena mai wake kuti, “Mwabala chiyani?” Chauta, Woyera uja wa Israele ndiponso Mlengi wake, akunena kuti, “Kodi iwe ungandifunse za ana anga, kapena kundilamula pa zokhudza ntchito zanga? Ndine amene ndidalenga dziko lapansi ndi kulenga munthu kuti akhalemo. Ndidayalika zakuthambo ndi manja anga, ndipo tsopano ndimalamulira gulu lonse lamumlengalenga. Ndine amene ndidautsa Kirusi kuti chilungamo chichitike. Ndidzaongola mseu uliwonse umene adzadzeramo. Adzamanganso mzinda wanga wa Yerusalemu ndi kumasula anthu anga amene ali mu ukapolo, osapereka ndalama kapena mphotho,” watero Chauta Mphambe. Chauta akuuza Aisraele kuti, “Chuma cha ku Ejipito ndi malonda a ku Etiopiya zidzakhala zanu. Anthu a ku Saba, a msinkhu aatali, adzabwera kwa inu ndi kukhala akapolo anu ndipo azidzakutsatani. Adzabwera ali omangidwa ndi maunyolo, ndi kukugwadirani. Adzakupembani ndi kunena kuti, ‘Mulungu ali ndi inu nokha, palibenso wina ai. Kupatula Iyeyo palibe mulungu wina. Ndithu inu muli ndi Mulungu wobisika, amene ali Mulungu wa Israele ndiponso Mpulumutsi. Onse amene amapanga mafano, adzaŵachititsa manyazi ndi kunyozetsa, adzamwazikana atasokonezeka. Koma Israele amampulumutsa ndi Chauta, ndipo chipulumutso chake chidzakhalapo mpaka muyaya, Anthu ake sadzaŵachititsa manyazi konse, sadzakhala onyozeka konse.’ ” Akutero Chauta amene adalenga zakumwamba, ndi Iyeyo Mulungu amene adaumba ndi kulenga dziko lapansi, ndipo adalikhazikitsa mwamphamvu. Sadalipange kuti likhale lopanda kanthu, koma kuti likhale malo okhalamo anthu. Iyeyo akunena kuti: “Chauta ndine, palibenso wina ai. Sindidalankhule mwachinsinsi pa malo ena m'dziko lamdima. Sindidauze zidzukulu za Yakobe kuti zizindifunafuna kumene kuli kopanda kanthu. Ine Chauta ndimalankhula zoona, ndimanena zolungama.” Chauta akuti, “Musonkhane pamodzi ndipo mubwere. Musendere pafupi, inu nonse amene mudapulumuka kwa anthu a mitundu ina! Ndi opanda nzeru amene amanyamula mafano amitengo, namapemphera kwa milungu imene singathe kuŵapulumutsa. Kambani, fotokozani mlandu wanu. Mupatsane nzeru nonse pamodzi. Kodi ndani adaneneratu zimene zidzachitika? Ndani adaloseratu kalekale zimenezo? Kodi si Ineyo, Chautane? Ndithu, kupatula Ine palibe Mulungu wina, Mulungu wachilungamo ndi wopulumutsa. Palibenso wina aliyense kupatula Ine.” “Inu anthu onse a pa dziko lapansi, tembenukirani kwa Ine kuti mupulumuke. Paja Ine ndine Mulungu, palibenso wina ai. Ndalumbira dzina langa lomwe, pakamwa panga palankhula moona mau amene sadzasinthika konse, akuti, ‘Bondo lililonse lidzandigwadira, anthu onse adzalumbira potchula dzina langa.’ “Pokamba za Ine adzanena kuti, ‘Chilungamo ndiponso mphamvu zimapezeka mwa Chauta yekha. Onse amene ankamugalukira adzabwera kwa Iye ndipo adzachita manyazi. Koma mwa Chautayo zidzukulu zonse za Israele zidzapambana ndi kupeza ulemerero.’ ” Nayu Beli wapendekeka, Nebo waŵerama! Mafano ameneŵa a Babiloni aŵaika pa abulu ndi ng'ombe. Zinthu zimene kale munkanyamula ndinu, tsopano mukuziika ngati katundu wolemera pamsana pa nyama zotopa. Nyamazo zikuŵerama ndi kufuna kugwa naye katunduyo, sizikutha kumpulumutsa. Izo zomwe zikupita ku ukapolo. “Mundimvere, inu zidzukulu za Yakobe, inu nonse otsala a m'nyumba ya Israele. Ndakhala ndikukusamalani chibadwire chanu, ndidakunyamulani kuyambira m'mimba mwa amai anu. Mpaka mudzakalambe ndidzakhalabe Yemwe uja, mpaka mudzamere imvi ndidzakusamalani ndithu. Ndidakulengani, ndipo ndidzakunyamulani. Ndidzakusenzani ndipo ndidzakuwombolani. “Kodi Ine mungandifanizire ndi yani, kapena kundilinganiza ndi yani? Kodi mungandiyerekeze ndi yani, kuti Ine ndi iyeyo tikhale ofanana? Anthu ena amatsekula zikwama zao namatulutsamo golide, ndipo amayesa siliva pa masikelo. Amalemba mmisiri wosula, ndipo iye amaŵapangira milungu. Kenaka iwowo amagwada pansi, namaipembedza milunguyo. Amainyamula pa mapewa ao, naisenza. Amaikhazika pamalo pake nikhala pomwepo, ndipo singathe kusuntha pamalo pakepo. Wina aliyense akapemphera kwa milunguyo, siyankha, kapena kumpulumutsa ku mavuto ake. “Mukumbukire zimenezi ndi kuganizapo, muzilingalire, inu ochimwanu. Mukumbukire zamakedzana zija. Mulungu ndine ndekha, palibenso wina ai. Ndithudi, Mulungu ndine, ndipo palibenso wina wonga Ine. Ndidaneneratu zakumathero kuchokera pa chiyambi pomwe. Kuyambira kalekale ndidaloseratu zimene zidakali zosachitikabe. Ndidaanena kuti, ‘Maganizo anga sadzalephera, ndidzachitadi zonse zimene ndidafuna kuchita.’ Ndikuitana chiwombankhanga kuchokera kuvuma, ndiye kuti munthu wofumira ku dziko lakutali, amene adzapherezetsa zimene ndikufuna kuchita. Zimene ndalankhula, ndidzazifitsa, zimene ndafuna kuchita ndidzazichitadi. “Mundimvere, inu ouma mitunu, inu amene muli kutali ndi chipulumutso. Tsiku la chipulumutso ndalisendeza pafupi, layandikira, sindidzachedwa kukupulumutsani. Ndidzapulumutsa Ziyoni, ndipo ndidzapatsa dziko la Israele ulemerero.” Chauta akunena kuti, “Iwe namwali, Babiloni, tsika ndi kukhala pa fumbi. Iwe namwali, Kaldeya, khala pansi, opanda mpando waufumu. Pakuti sadzakutchulanso wofeŵa ndi wodzitekemeza. Tenga mphero kuti upere ufa. Chotsa nsalu yako yakumaso. Kwinda zovala zako mpaka m'ntchafu, woloka mitsinje. Maliseche ako adzakhala poyera, ndipo udzachita manyazi kwambiri. Ndidzalipsira, ndipo palibe amene adzandiletsa.” Woyera uja wa Israele ndiye Mpulumutsi wathu, dzina lake ndi Chauta Mphambe. Akuuza Babiloni kuti, “Khala chete ndi kuloŵa mu mdima, iwe namwali, Kaldeya. Sadzakutchulanso mfumukazi ya maufumu. Ndidaŵakwiyira anthu anga, ndidaŵanyoza ngati si anthu anga. Ndidaŵapereka m'manja mwako, ndipo iwe sudaŵachitire chifundo. Udaumira mtima ndi nkhalamba zomwe. Unkaganiza kuti nthaŵi zonse udzakhala mfumukazi, mwakuti zinthu zimenezi sudazisamale, sudaganizirenso m'mene zidzathere.” “Nchifukwa chake tsono umvetsere izi, iwe wongokonda zokondweretsawe, iwe amene umakhala pabwino, numaganiza mumtima mwako kuti, ‘Ndi ineyo basi, kupatula ine palibenso wina ai. Sindidzakhala konse wamasiye, ndipo ana anga sadzafa.’ ” Koma m'kamphindi, tsiku limodzi, zinthu ziŵiri zonsezi zidzakugwera. Ana ako onse kukufera, iweyo kusanduka wamasiye, zonsezo zidzakugwera pamodzi, ngakhale kuti uli ndi matsenga ambiri ndi zithumwa zamphamvu. “Sunkada nako nkhaŵa konse kuipa kwako, unkaganiza kuti palibe wokupenya. Kuchenjera kwako ndi nzeru zako zidakusokeza, ndipo mumtima mwako unkaganiza kuti, ‘Ndi ineyo basi, kupatula ine palibenso wina ai.’ ” Tsoka lidzakugwera, ndipo sudzatha kuliletsa ndi matsenga ako. Chiwonongeko chidzakufikira, iwe osatha kuchithaŵa, chipasupasu chosayembekezeka konse chidzakugwera mwadzidzidzi. Khala nazo nyanga zako ndi matsenga ako. Wakhala ukuzigwiritsa ntchito chiyambire cha ubwana wako. Mwina mwake zingakuthandize kapena nkuwopsa nazo adani ako. Udangodzitopetsa nako kupempha malangizo ambiri. Nabwere okulangizawo kuti adzakupulumutse. Abweretu anthu amene amaphunzira zakumlengalenga, namayang'ana nyenyezi, amenenso amati mwezi ukakhala nkumalosa zimene zidzakuchitikira. “Taona, anthuwo ali ngati mapesi, adzapsa ndi moto. Sangathe kudzipulumutsa ku mphamvu ya malaŵi ake. Moto wake si woti nkuwotha kapena kusendera pafupi nawo ai. Ndimo m'mene adzakuthandizire anthuwo amene wakhala ukugwira nao ntchito ndi kuchita nao malonda chiyambire cha ubwana wako. Onsewo adzangomwazikana, sipadzakhala ndi mmodzi yemwe wokupulumutsa.” Mverani izi inu a banja la Yakobe, inu amene dzina lanu amakutchulani Aisraele, inu zidzukulu za Yuda. Inu mumalumbira dzina la Chauta, ndipo mumapemphera kwa Mulungu wa Israele, pamene zimenezo sizichokera mu mtima woona ndi wolungama. Komabe inu mukunyada kuti ndinu nzika za mzinda wopatulika ndipo kuti mumakhulupirira Mulungu wa Israele, amene dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse. Chauta akuuza Israele kuti, “Zimene zidachitika poyamba ndidaaloseratu kalekale, zidaatuluka m'kamwa mwanga, ndipo ndidaazilengeza. Tsono mwadzidzidzi ndidachitapo kanthu, ndipo zidaonekadi. Ndidaadziŵa kuti ndiwe wokanika, wa nkhongo gwa, ndi wa mutu wouma. Ndidaakuuziratu zakutsogolo kalekale. Zisanachitike ndidaazilengezeratu kwa iwe, kuti usadzanene kuti, ‘Fano langa ndilo lidachita zimenezi, fano langa losema ndi fano langa loumba ndiwo adalamula kuti zichitike!’ “Zonsezi udazimva, tsono uzilingalire bwino. Monga iweyo sungazivomereze? Kuyambira tsopano mpaka m'tsogolo muno ndidzakuuza zinthu zatsopano, zinthu zobisika zimene sudazidziŵe konse. Zinthu zimenezi zikulengedwa tsopano lino, osati kalekale. Mpaka lero unali usanazimve konse, kuwopa kuti ungamati, ‘Zimenezi ndiye ai, ndidazidziŵa kale.’ Chikhalire sudamve chikhalire sudadziŵe, nkale lonse makutu ako sanali otsekuka. Chifukwa ndidaadziŵa kuti ndiwe wachiwembu, ndipo kuti chiyambire cha ubwana wako adakutchula waupandu. “Kuti anthu alemekeze dzina langa ndikuchedwetsa mkwiyo wanga. Kuti anthu aone ulemerero wanga ndikukulezera ukali wanga, kuti ndisakuwononge kotheratu. Ndidakuyeretsa, komatu osati ngati siliva, ndidakuyesa m'ng'anjo yamasautso. Chifukwa cha ulemu wanga, ulemu wanga wokha, ndiye ndimachita zonse. Ndingalole bwanji kuti dzina langa linyozeke? Ulemerero wanga sindidzapatsa wina ai.” Chauta akunena kuti, “Mverani Ine, inu zidzukulu za Yakobe, inu Aisraele, amene ndidakuitanani. Mulungu uja ndine, ndine woyamba ndipo ndine wotsiriza. Manja anga adamanga maziko a dziko lapansi, dzanja langa lamanja lidafunyulula mlengalenga. Ndikaitana dziko lapansi ndi dziko lakumwamba, zonsezo zimabwera pamodzi kwa Ine. “Sonkhanani nonsenu, ndipo mumvetsere. Mwa milungu ina ndani adalosapo zimenezi? Amene Chauta amamkonda uja adzachita zomwe Chautayo adakonzera Babiloni, ndi dzanja lake lamphamvu adzalimbana ndi Akaldeya. Ndine amene ndidalankhula ndi kumuitana. Ndidambweretsa ndine, ndipo zonse zidzamuyendera bwino. Bwerani pafupi tsono, kuti mumve zimene nditi ndinene. Kuyambira pa chiyambi sindidalankhule mobisa, nthaŵi imene zimenezo zinkachitika, nkuti Ine ndilipo.” Tsono Ambuye Chauta andipatsa Mzimu wao, ndipo andituma. Chauta, Mpulumutsi wako, Woyera uja wa Israele, akunena kuti, “Ine ndine Chauta, Mulungu wako, amene ndimakuphunzitsa, kuti zinthu zikuyendere bwino. Ndimakutsogolera pa njira yoyenera kuitsata. Ukadamvera malamulo anga, bwenzi mtendere ukukufikira ngati madzi amumtsinje, ndipo bwenzi chilungamo chikukuphimba kosalekeza ngati mafunde apanyanja. Ana ako akadachuluka ngati mchenga, ndipo zidzukulu zako ngati fumbi. Dzina lao silikadachotsedwa pamaso panga, silikadafafanizika konse. “Tulukani m'dziko la Babiloni, thaŵani m'dziko la ukapolo. Mulengeze zimenezi ndi mau amphamvu, muzilalike, muzifikitse mpaka ku mathero a dziko lapansi. Muzinena kuti, ‘Chauta waombola Yakobe, mtumiki wake.’ ” Pamene ankatsogolera anthu ake m'chipululu, iwo sadamve ludzu. Adaŵapatsa madzi otuluka m'thanthwe. Adang'amba thanthwelo, ndipo mudatuluka madzi. “Koma anthu ochimwa alibe mtendere,” akuterotu Chauta. Mverani inu anthu a ku maiko a m'mphepete mwa nyanja, tcherani khutu, inu anthu akutali. Chauta adandiitana ndisanabadwe, adanditchula dzina ndidakali m'mimba mwa amai anga. Adasandutsa pakamwa panga kuti pakhale ngati lupanga lakuthwa. Adanditchinjiriza ndi dzanja lake. Adandisula ngati muvi wakuthwa, nandibisa m'phodo mwake. Adandiwuza kuti, “Iwe Israele ndiwe mtumiki wanga. Anthu adzanditamanda chifukwa cha iwe.” Koma ndidati, “Ndagwira ntchito yopanda phindu. Ndangoononga mphamvu zanga pachabe.” Komabe zondiyenerera zili m'manja mwa Chauta, mphotho yanga ili m'manja mwa Mulungu wanga. Chauta ndi amene adandiwumba m'mimba mwa amai anga kuti ndikhale mtumiki wake, kuti ndibweze fuko la Yakobe kwa Iye, ndipo kuti ndisonkhanitse Aisraele pafupi ndi Iye. Choncho ndimalemekezeka m'maso mwa Chauta, ndimapeza mphamvu mwa Mulungu wanga. Chautayo akunena kuti, “Nchinthu chochepa kwambiri kuti ukhale mtumiki wanga, kuti udzutse mafuko a Yakobe ndi kuŵabweza kwao Aisraele amene adapulumuka. Ndidzakusandutsa kuŵala kounikira mitundu ina ya anthu, kuti chipulumutso changa chikafike mpaka ku mathero a dziko lapansi.” Chauta, Mpulumutsi ndi Woyera uja wa Israele, akulankhula ndi wonyozedwa kwambiri uja, wodedwa ndi mitundu ina ya anthu, kapolo wa mafumu ankhanza. Akunena kuti, “Mafumu adzaimirira mwaulemu poona iwe, akalonga nawonso adzadziponya pansi chafufumimba. Zimenezi zidzachitika chifukwa cha Chauta, amene ali wokhulupirika, Woyera uja wa Israele, amene adakusankhula.” Chauta akunena kuti, “Nthaŵi imene ndidakukomera mtima, ndidakuyankha, ndipo tsiku la chipulumutso ndidakuthandiza. Ndidakusunga ndipo ndidakusandutsa kuti ukhale chipangano kwa anthu, kuti ndilibwezere dziko mwakale ndi kuligaŵagaŵa dziko loonongekali. Ndidzauza am'ndende kuti atuluke, ndi amene ali mu mdima kuti aonekere poyera. Adzapeza chakudya m'mphepete mwa njira, adzapeza busa pa magomo. Sadzamva njala kapena ludzu. Mphepo yotentha kapena dzuŵa sizidzaŵapsereza, chifukwa amene amaŵachitira chifundo adzaŵatsogolera ndi kuŵaperekeza ku akasupe a madzi. Mapiri anga onse ndidzaŵasandutsa njira yoyendamo, ndipo miseu yanga yaikulu ndidzaikonza. Onani, anthu anga adzachokera kutali, ena kumpoto, ena kuzambwe, enanso adzachokera ku Asuwani kumwera.” Imbani mokondwa, inu zolengedwa zamumlengalenga! Fuula ndi chimwemwe, iwe dziko lapansi! Yambani nyimbo, inu mapiri! Chauta watonthoza mtima anthu ake, ndi kuŵamvera chifundo anthu ake ovutika. Koma anthu a ku Ziyoni adati, “Chauta watisiya ife, Ambuye atiiŵala.” Apo Chauta adafunsa kuti, “Kodi mkazi angathe kuiŵala mwana wake wapabere, osamumvera chifundo mwana wobala iye yemwe? Ndipotu angakhale aiŵale mwana wake, Ine ai, sindidzakuiŵalani konse. Iwe Yerusalemu, ndidadinda chithunzi chako pa zikhatho zanga, zipupa zako ndimakhala ndikuziwona nthaŵi zonse. Amisiri odzakumanganso akubwera mofulumira, ndipo okupasula ndi okuwononga akuchokapo. Uyang'ane pozungulira, uwone zimene zikuchitika. Anthu ako onse akusonkhana, akubwera kwa iwe. Pali Ine ndemwe, Mulungu wamoyo, anthu ako adzakhala chinthu chokukongoletsa. Udzaŵaonetsera monga amachitira mkwati wamkazi. Ndithudi, iwe amene wasanduka bwinja, amene udaasiyidwa ndi kusakazika, tsopano udzaŵachepera anthu odzakhala mwa iwe. Ndipo amene adakuwononga aja adzaŵapirikitsira kutali ndi iwe. Ana ako obadwa pa nthaŵi yako yachisoni adzakuneneranso m'khutu mwako kuti, ‘Dziko likutichepera, utikulitsire malo oti tizikhalapo.’ Tsono iwe udzadzifunsa kuti, ‘Kodi ndani adandiberekera ana aŵa? Ana anga onse adamwalira ndipo sindidanthenso kukhala ndi ana ena. Ndidaali ku ukapolo, ndidaaiŵalika. Nanga ndani adaŵalera ana ameneŵa? Ndidaatsala ndekha. Nanga ana ameneŵa adachokera kuti?’ ” Ambuye Chauta akunena kuti, “Ndidzakodola anthu a mitundu ina. Ndidzaŵakwezera mbendera kuti adzabwere. Tsono adzabwera nawo ana ako aamuna ataŵatengera m'manja, ndiponso ana ako aakazi, ataŵasenzera pa mapewa. Mafumu adzakhala ngati atate okulerani, akazi a mafumuwo adzakhala ngati amai okuyamwitsani. Adzagwetsa nkhope zao pansi ndi kukuŵeramirani. Adzaseteka fumbi la m'mapazi mwanu modzichepetsa. Pamenepo mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndipo amene amakhulupirira Ine sadzachita manyazi.” Kodi mungathe kuŵalanda ankhondo zofunkha zao? Kodi mungathe kuŵapulumutsa akaidi kwa mfumu yankhalwe? Chauta akuyankha kuti, “Ndithudi, ankhondo adzaŵalanda akaidi ao, ndipo mfumu yankhalwe adzailanda zofunkha zake. Ndidzalimbana ndi amene amalimbana nanu, ndipo ndidzapulumutsa ana anu. Ndidzaumiriza okuzunzani kuti adzadye mnofu wao womwe. Ndipo adzaledzera nawo magazi ao omwe, monga momwe adakachitira ndi vinyo watsopano. Motero anthu onse adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, Mpulumutsi wanu, ndine Momboli wanu, Wamphamvu uja wa Yakobe.” Chauta akuti, “Ili kuti kalata yake imene ndidasudzulira mai wanu? Mwa anthu amene ndili nawo ndi ngongole, ndidakugulitsani kwa uti? Iyai, inutu mudagulitsidwa ku ukapolo chifukwa cha machimo anu, ndipo mai wanu adachotsedwa chifukwa cha upandu wanu. Chifukwa chiyani panalibe anthu, pamene ndidabwera kudzaŵapulumutsa? Chifukwa chiyani panalibe wondiyankha, pamene ndidaitana? Kodi dzanja langa nloti nkulephera kuwombola? Kodi kapena ndilibe mphamvu zopulumutsira? Nditangodzudzula chabe, nyanja yaikulu itha kuuma, ndipo mitsinje itha kusanduka chipululu. Chifukwa chosoŵa madzi nsomba zam'menemo nkuyamba kununkha, ndiponso kufa ndi ludzu. Nditha kuphimba thambo ndi mdima, ndi kulisandutsa ngati likulira maliro.” Ambuye Chauta andiphunzitsa zoyenera kunena, kuti ndidziŵe mau olimbitsa mtima anthu ofooka. M'maŵa mulimonse amandidzutsa, amathwetsa makutu anga kuti ndimve, monga amachitira amene akuphunzira. Ambuye Chauta anditsekula makutu, ndipo sindidaŵanyoze kapena kuŵapandukira. Ndidaperekera msana wanga kwa ondimenya, ndiponso masaya anga kwa ondimwetula ndevu. Sindidaŵabisire nkhope ondinyoza ndi ondithira malovu. Koma kunyoza kwao sindikuvutika nako, chifukwa Ambuye Chauta amandithandiza. Nchifukwa chake ndalimbitsa mtima wanga ngati mwala. Ndikudziŵa kuti sadzandichititsa manyazi. Wondikhalira kumbuyo ali pafupi, ndaninso angandiimbe mlandu? Tipitire limodzi ku bwalo lamilandu. Wofuna kutsutsana nane ndani? Nabwere pafupi. Ambuye Chauta ndi amene amandithandiza, ndani anganene kuti ndine wopalamula? Ndithu, onse ondizenga mlandu adzatheratu. Kutha kwake ngati chovala chodyewa ndi njenjete. Ndani mwa inu amaopa Chauta, ndi kumvera mau a mtumiki wake? Aliyense woyenda mu mdima, wopanda chomuunikira, akhulupirire dzina la Chauta, ndipo adalire Mulungu wake. Nonsenu amene mumasonkha moto ndi kuyatsa zikuni kuti muwononge anzanu, loŵani inuyo m'moto wanu womwewo, yendani pakati pa zikuni zimene mudayatsazo. Mudzakhala m'mazunzo, ndipo ndi Ineyo Chauta amene ndidzagwetsa mazunzowo. Chauta akunena kuti: “Tcherani khutu inu amene mufuna kupulumuka, inu amene mufuna kuti ndikuthandizeni. Taganizani za thanthwe kumene mudasemedwa, ku nkhuti ya miyala kumene adakukumbani. Taganizani za Abrahamu, bambo wanu ndi Sara amene adakubalani. Pamene ndinkamuitana Abrahamu, adaalibe mwana. Koma ndidamudalitsa, ndidampatsa ana, ndipo ndidachulukitsa zidzukulu zake. Ndidzatonthoza mtima Ziyoni, ndidzaŵatonthoza mtima okhala ku mabwinja ake. Ngakhale dziko lake ndi chipululu, ndidzalisandutsa ngati Edeni. Ngakhale dziko lake ndi thengo, ndidzalisandutsa ngati munda wa Chauta. Kumeneko anthu adzakondwa ndi kusangalala, adzaimba nyimbo zondilemekeza ndi zondithokoza. “Mverani, inu anthu anga, tcherani khutu, inu mtundu wanga. Malamulo adzachokera kwa Ine, ndipo chilungamo changa chidzaunikira anthu onse. Ndidzabwera mofulumira kudzaombola anthu anga, nthaŵi yanga ya kuŵapulumutsa ili pafupi. Ine mwiniwakene ndidzalamulira mitundu ya anthu onse. Maiko akutali akundidikira kuti ndibwere, akundiyembekeza ndi chikhulupiriro kuti ndidzaŵapulumutse. Yang'anani mlengalenga, yang'anani dziko lapansi. Mlengalenga udzazimirira ngati utsi, dziko lapansi lidzatha ngati chovala, ndipo anthu ake onse adzafa ngati ntchentche. Koma chipulumutso changa chidzakhala mpaka muyaya, ndipo kuwombola kwanga kudzakhala kwa nthaŵi zonse. “Mverani, inu amene mukudziŵa chilungamo, inu amene mukusunga malamulo anga mumtima mwanu. Musachite mantha anthu akamakudzudzulani, musataye mtima akamakulalatirani. Anthu otereŵa adzatha ngati nsalu yodyewa ndi njenjete, adzatha ngati thonje lodyewa ndi mbozi. Koma chipulumutso changa chidzakhala mpaka muyaya, kuwombola kwanga kudzakhala kwa nthaŵi zonse.” Dzambatukani, Inu Chauta, dzambatukani! Valani dzilimbe. Dzambatukani monga momwe munkachitira masiku amakedzana, nthaŵi ya mibadwo yakale. Kodi sindinu uja mudaduladula Rahabu, chilombo cham'nyanja chija, ndi kubaya chinjoka cham'nyanja chija? Kodi sindinu amene mudaumitsa nyanja yaikulu ija, madzi ozama kwambiri? Kodi sindinu amene mudapanga njira pa madzi, kuti amene mudaŵapulumutsa aoloke pouma. Amene mudaŵaombola adzabwerera, ndipo adzafika ku Ziyoni nyimbo ili pakamwa. Chimwemwe chamuyaya chizidzaonekera pankhope pao. Adzakhala ndi chikondwerero ndi chisangalalo. Chisoni ndi kubuula zidzatha. Chauta akunena kuti, “Ineineyo ndine amene ndimakutonthozani mtima. Kodi ndinu yani kuti muziwopa munthu woti adzafa, mwanawamunthu amene angokhala nthaŵi yochepa ngati udzu? Kodi ndinu yani kuti muziiŵala Chauta, Mlengi wanu, amene adayalika zakuthambo, ndi kuika maziko a dziko lapansi? Kodi ndinu yani kuti nthaŵi zonse muziwopa ukali wa anthu okuzunzani, amene angofuna kukuwonongani? Ukali wa anthu okuzunzaniwo tsopano uli kuti? Am'ndende adzaŵamasula posachedwa. Sadzafa, sadzaloŵa m'manda, ndipo chakudya sichidzaŵasoŵa konse. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu, amene ndimavundula nyanja, kotero kuti mafunde ake amakokoma. Dzina langa ndine Chauta Wamphamvuzonse. Ndidaika mau anga m'kamwa mwanu, ndipo ndidakutetezani ndi dzanja langa. Ndidayalika zakuthambo, ndi kukhazika maziko a dziko lapansi. Ndidauza anthu a ku Ziyoni kuti, ‘Ndinu anthu anga.’ ” Dzuka, dzuka, imirira, iwe Yerusalemu. Wamwa chikho chachilango chimene Chauta adakupatsa ali wokwiya. Chikhocho nchochititsa chizwezwe, ndipo iwe udachigugudiza. Palibe wina wokutsogolera mwa ana amene udaŵabala. Palibe ndi mmodzi yemwe wokugwira pa dzanja mwa ana amene udaŵalera. Mavuto akugwera paŵiri: dziko lako lasakazika ndi kuwonongeka, ndipo anthu ako apululuka ndi njala ndi nkhondo. Ndani angakumvere chifundo? Ndani angakutonthoze mtima? Ana ako akomoka, ali ngundangunda pa miseu yonse ngati mphoyo zokodwa mu ukonde. Kwaŵagwera kukwiya kwa Chauta ndi kudzudzula kwake. Nchifukwa chake imva iwe amene ukuvutika, iwe amene waledzera, koma osati ndi vinyo. Chauta, Ambuye ako, Mulungu wako, amene amakutchinjiriza, akunena kuti, “Ona, ndakulanda chikho chochititsa chizwezwe chija. Chikhocho, chimene ndidakupatsani ndili wokwiya, sudzachimwanso. Chikhocho ndidzachipereka kwa okuzunza, amene adaakuuza kuti, ‘Gona pansi, tikuyende pamsana.’ Msana wako adauyesa pansi popondapo, adauyesa mseu woti ayendepo.” Dzuka, dzuka, vala dzilimbe iwe Ziyoni. Vala zovala zako zabwino, iwe Yerusalemu, mzinda woyera. Anthu osaumbalidwa ndi onyansa pa chipembedzo sadzaloŵanso pa zipata zako. Udzisanse fumbi ndipo udzuke, iwe Yerusalemu wogwidwa. Inu omangidwa a ku Ziyoni, aduleni maunyolo ali m'khosi mwanuwo. Chauta akunena kuti, “Sadalandirepo kanthu pokugulitsani, choncho mudzaomboledwa osaperekapo ndalama. Kale inu anthu anga mudaapita ku Ejipito kukakhala nao kumeneko, ndipo Aasiriya adaakuzunzani popanda chifukwa. Tsono Ine Chauta ndikunena kuti, ‘Tsopano nditani poona kuti anthu anganu adakutengani ukapolo osaperekapo kanthu? Okulamulani akufuula monyodola, ndipo angokhalira kundinyoza kosalekeza. Pamenepo inu anthu anga mudzandidziŵa, nthaŵi imeneyo mudzadziŵa kuti ndine amene ndikulankhula. Ndithu ndinedi!’ ” Si kukondwetsa kwake pamene mukuwona wamthenga akuyenda m'mapiri, akubwera ndi uthenga wabwino, akulengeza za mtendere, akudzetsa chisangalalo, akulengeza za chipulumutso, akuuza anthu a ku Ziyoni kuti, “Mulungu wanu ndi mfumu.” Mverani, alonda anu akukweza mau, akuimba pamodzi mokondwa, popeza kuti akuwona chamaso Chauta akubweranso ku Ziyoni. Fuulani mokondwera inu mabwinja a Yerusalemu, pakuti Chauta waŵatonthoza mtima anthu ake, wapulumutsa Yerusalemu. Chauta wagwiritsa ntchito mphamvu zake zoyera pamaso pa anthu a mitundu yonse, dziko lonse lapansi mpaka ku mathero lidzaona chipulumutso cha Mulungu wathu. Nyamukani, nyamukani, chokaniko msanga ku Babiloniko, musakhudze kanthu konyansa pa chipembedzo. Tulukanimo ndipo mudziyeretse, inu amene mukunyamula ziŵiya zopatulikira Chauta. Koma ulendo uno simudzachoka mofulumira, simudzachita chothaŵa. Chauta azidzayenda patsogolo panu, Mulungu wa Aisraele azidzakutetezani kumbuyo kwanu. Chauta akuti, “Mtumiki wanga adzapambana pa ntchito yake. Adzakwezedwa ndi kulemekezedwa, ndipo adzalandira ulemu waukulu kwambiri. Anthu ambiri atamuwona adadzidzimuka, chifukwa nkhope yake inali itasakazika, kotero kuti siinkachitanso ngati ya munthu. Maonekedwe ake sanalinso ngati a munthu. Chimodzimodzinso anthu a mitundu yonse adzadodoma naye, Mafumu omwe adzasoŵa naye chonena, popeza kuti zinthu zosaŵauzapo chiyambire adzaziwona, ndipo zinthu zosamvapo nkale lonse, adzazimvetsa.” “Ndani wazikhulupirira zimene tamvazi? Ndani wazindikira mphamvu za Chauta pa zimenezi? Pajatu mtumiki wake uja adakula ngati chiphukira pamaso pa Mulungu, ndiponso ngati muzu m'nthaka youma. Iye analibe maonekedwe enieni kapena nkhope yabwino, kuti ife nkumamuyang'ana. Analibe kukongola koti ife nkukokeka naye. Iye uja anthu adamnyoza ndipo adamkana. Anali munthu wamasautso, wozoloŵera zoŵaŵa. Anali ngati munthu amene anzake amaphimba kumaso akamuwona. Anthu adamnyoza, ndipo ife sitidamuyese kanthu. “Ndithudi, iye adapirira masautso amene tikadayenera kuŵamva ifeyo, ndipo adalandira zoŵaŵa zimene tikadayenera kuzilandira ifeyo. Koma ife tinkaganiza kuti ndi Mulungu amene akumlanga, ndi kumkantha ndi kumsautsa. Koma adambaya chifukwa cha machimo athu, ndipo adamtswanya chifukwa cha zoipa zathu. Chilango chimene chidamgwera iye chatipatsa ife mtendere, ndipo mabala ake atichiritsa. Tonse tidaasokera ngati nkhosa. Aliyense mwa ife ankangodziyendera. Ndipo Chauta adamsenzetsa iyeyo machimo athu. “Anthu adamsautsa ndi kumzunza, koma iye sadalankhule kanthu. Monga momwe amachitira mwanawankhosa wopita naye kuti akamuphe, ndiponso monga momwe nkhosa imakhalira duu poimeta, nayenso adangokhala chete. Adamgwira mwankhanza namuzenga mlandu, ndipo adapita naye kukamupha. Mwa anthu anzake ndani adalabadako zoti iye adachotsedwa m'dziko la anthu amoyo? Ndani adalabadako kuti iye uja adalangidwa chifukwa cha machimo a anthu? Adamkonzera manda ake pakati pa manda a achifwamba. Adamuika m'manda pakati pa anthu olemera, ngakhale iye sadachitepo chosalungama chilichonse ndipo sadanene bodza lililonse.” Komabe ndi Chauta yemwe amene adaafuna kuti amuzunze, ndipo adamsautsadi. Iye adapereka moyo wake kuti ukhale nsembe yokhululukira machimo. Choncho adzaona zidzukulu zake, adzakhala ndi moyo wautali, ndipo chifuniro cha Chauta chidzachitika mwa iye. Atatha mazunzo akewo, adzaona phindu lake, ndipo adzakhutira. Mwa nzeru zake mtumiki wanga wolungamayo adzasenza machimo a anthu onse kuti iwo ambiri a iwo asadzapezekenso kuti ndiopalamula. Motero Ine ndidzampatsa ulemu woyenerera akuluakulu. Adzagaŵana zofunkha ndi ankhondo amphamvu, popeza kuti adapereka moyo wake mpaka kufa, ndipo adamuyesa mnzao wa anthu ophwanya malamulo. Adasenza machimo a anthu ambiri, ndipo adaŵapempherera ochimwawo kuti akhululukidwe. “Fuula ndi chimwemwe iwe Yerusalemu amene wakhala ngati chumba chopanda ana, fuula mosangalala, iwe amene sudamvepo zoŵaŵa za kubala. Pakuti tsopano udzakhala ndi ana ochuluka kuposa mkazi amene sadasiyidweko ndi mwamuna wake,” akuterotu Chauta. “Ukuze malo omangapo hema lako, ufunyulule kwambiri nsalu zake. Usalephere, utalikitse zingwe zake, ndipo ulimbitse zikhomo zake. Udzasendeza malire ake uku ndi uku. Zidzukulu zako zidzalanda dziko la anthu a mitundu ina, zidzadzaza mizinda imene idasiyidwa. “Usaope, chifukwa sadzakunyozanso, usataye mtima poti sadzakupeputsanso. Udzaiŵala zimene zidakuchititsa manyazi pa unyamata wako, manyazi a pa umasiye wako sudzaŵakumbukanso. Mlengi wako ali ngati mwamuna wako. Chauta Wamphamvuzonse ndiye dzina lake. Woyera Uja wa Israele ndiye Momboli wako, dzina lake ndi Mulungu wa dziko lonse lapansi. Iwe Israele, Chauta wakuitananso. Uli ngati msungwana wosiyidwa, amene ali wodzaza ndi chisoni mu mtima, ngati mkazi wapaunyamata amene wachotsedwa, akuterotu Mulungu wako.” “Ndidaakusiya pa kamphindi kochepa, koma ndidzakutenganso ndi chikondi chachikulu. Ndidaakufulatira pa mphindi yaing'ono ndili wokwiya zedi, koma ndidzakuwonetsa chikondi changa mpaka muyaya,” akuterotu Chauta, Momboli wako. “Kwa ine zimenezi zili monga m'mene zinaliri nthaŵi ya Nowa: monga momwe ndidaalumbirira nthaŵi imeneyo kuti sindidzaononganso dziko lapansi ndi chigumula, chonchonso tsopano ndikulumbiranso kuti sindidzakupseranso mtima, ndipo sindidzakudzudzulanso. Mapiri angathe kusuntha, magomo angathe kugwedezeka, koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha. Lonjezo langa losunga mtendere mpaka muyaya silidzatha,” akuterotu Chauta amene amakumvera chifundo. Chauta akunena kuti, “Iwe Yerusalemu ndiwe mzinda wozunzika, wosoŵa chithandizo, wopanda wokutonthoza. Ndidzakongoletsa miyala yako, ndidzamanganso maziko ako ndi miyala ya mtengo wapatali. Ndidzamanga nsanja zako ndi miyala yofiira. Ndidzamanga zipata zako ndi miyala yochezimira ngati moto. Ndidzamanganso linga lokuzungulira ndi miyala ya mtengo wapatali. Anthu ako ndidzaŵaphunzitsa ndekha, Ine Chauta, ana ako ndidzaŵadalitsa ndi kuŵapatsa mtendere waukulu. Udzakhazikika m'chilungamo chenicheni. Sudzakhalanso wopanikizika, chifukwa palibe choopa, sudzakhalanso ndi mantha, chifukwa manthawo sadzakufikira. Ngati wina autsa nkhondo, si ndine ndachititsa ai. Amene alimbana nawe adzalephera, poti udzaŵagonjetsa. Udziŵe kuti ndidalenga ndine munthu wosula, amene amakoleza moto wamakala kuti asulire zida. Ndidalenganso ndine munthu wosakaza kuti aononge. Koma iwe palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke. Onse okuneneza udzaŵatsutsa. Ndimo adzapezera atumiki anga, ndipo ndidzaŵapambanitsa ndine,” akuterotu Chauta. Chauta akunena kuti, “Inu nonse omva ludzu, bwerani, madzi ali pano. Ndipo inu amene mulibe ndalama, bwerani mudzagule chakudya, kuti mudye. Bwerani mudzagule vinyo ndi mkaka, osalipira ndalama, osalipira chilichonse. Chifukwa chiyani ndalama zanu mukuwonongera zinthu zimene saadya? Chifukwa chiyani malipiro anu mukuwonongera zinthu zimene sizingakuchotseni njala? Mvetsetsani zimene ndikunena Ine, ndipo muzidya zimene zili zabwino, muzidzisangalatsa ndi zakudya zonona. Tcherani makutu, ndipo mubwere kwa Ine. Mumvere Ine, kuti mukhale ndi moyo. Ndidzachita nanu chipangano chosatha, ndipo ndidzakuwonetsani chikondi chosasinthika ndi chosapeneka, chimene ndidaalonjeza Davide. “Mudziŵe kuti iye uja ndidamsankha kuti akhale mboni yanga kwa mitundu ya anthu, kuti akhale mtsogoleri ndi wolamulira anthu ambiri. Tsopano mudzaitana mitundu imene simuidziŵa. Mitundu imene sikudziŵani idzabwera ndi liŵiro kuti ikhale nanu, chifukwa cha Ine Chauta, Mulungu wanu, Woyera uja wa Israele, amene ndidakupatsani ulemerero.” “Mufunefune Chauta pamene angathe kupezeka, mupemphere kwa Iye pamene ali pafupi. Oipa asiye makhalidwe ao oipa, ndipo osalungama asinthe maganizo ao oipa. Abwerere kwa Chauta, kuti Iyeyo aŵachitire chifundo. Abwerere kwa Mulungu wathu, kuti Iye aŵakhululukire machimo ao mofeŵa mtima.” Chauta akunena kuti, “Maganizo anga ndi maganizo anu si amodzimodzi, ndipo zochita zanga ndi zochita zanu si zimodzimodzi. Monga momwe mlengalenga uliri kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu. “Mvula ndi chisanu chambee zimatsika kuchokera kumwamba, ndipo sizibwerera komweko, koma zimathirira nthaka. Zimameretsa ndi kukulitsa zomera, kenaka nkupatsa alimi mbeu ndi chakudya. Ndimonso amachitira mau ochokera m'kamwa mwanga. Sadzabwerera kwa Ine popanda phindu lake, koma adzachita zonse zimene ndifuna, ndipo zimene ndidaŵatumira zidzayenda bwino. “Inu anthu anga, mudzachoka ku Babiloni mokondwa, adzakutulutsani mumzindamo mwamtendere. Inu mukufika, mapiri ndi magomo adzakuimbirani nyimbo. Nayonso mitengo yonse yam'thengo idzakuwomberani m'manja. Kumene tsopano kuli mitengo yaminga kudzamera mitengo ya paini. Kumene tsopano kuli mkandankhuku kudzamera michisu. Zimenezi zidzakhala chikumbutso cha Ine Chauta, ngati chizindikiro chamuyaya chimene sichidzafafanizika konse.” Chauta akuuza anthu ake kuti, “Muzichita zabwino ndi zolungama, chifukwa ndikuwombolani posachedwa, chipulumutso changa chiwoneka.” Ndi wodala munthu amene amachita zimenezi, munthu amene amalimbikira kuzichita, amene amalemekeza tsiku la Sabata, osaliwononga, ndipo amadziletsa kuchita zoipa. Mkunja amene waphatikana ndi Chauta, asanene kuti, “Mosapeneka konse Chauta adzandichotsa pakati pa anthu ake.” Nayenso wofulidwa asanene kuti, “Ine ndiye ndine wouma ngati chikuni.” Paja Chauta akuti, “Ofulidwa amene amalemekeza masiku a Sabata, amene amachita zokomera Ine, ndi kusunga chipangano changa mokhulupirika, Ineyo ndidzaŵapatsa dzina ndi mbiri yabwino pakati pa anthu anga, m'kati mwa fuko langa, koposa kukhala ndi ana aamuna ndi aakazi. Ndidzaŵapatsa mbiri yabwino yosatha, yosaiŵalika.” Chauta akutinso, “Akunja amene amaphatikana ndi Chauta mpaka kumgwirira ntchito, kumkonda, ndi kumtumikira, amenenso amalemekeza tsiku la Sabata, osaliwononga, nasunga bwino chipangano changa, Ine ndidzaŵafikitsa ku Ziyoni, phiri langa lopatulika. Ndidzaŵapatsa chimwemwe m'nyumba yanga yopemphereramo. Zopereka zao zootcha ndiponso nsembe zao zinanso ndidzazilandira pa guwa langa. Paja Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo anthu a mitundu yonse.” Chauta, amene amasonkhanitsa Aisraele onse obalalika, akunena kuti, “Ndidzasonkhanitsanso anthu ena kuwonjezera pa amene adasonkhana kale.” Chauta akuuza anthu a mitundu ina kuti, “Inu nonse zilombo zakuthengo, nonse zilombo zam'nkhalango, bwerani mudzadye. Atsogoleri onse a Israele ndi akhungu, onsewo ndi opanda nzeru konse. Ali ngati agalu opanda mau, osatha kuuwa. Ntchito nkulota, kugona pansi, kukondetsa tulo. Ali ngati agalu a njala yaikulu, amene sakhuta konse. Abusa nawonso ndi opanda nzeru. Aliyense amachita monga m'mene afunira, ndipo amangofuna zokomera iye yekha. Zidakwa zimenezi zimati, ‘Tiyeni timwe vinyo, tiyeni timwe zakumwa zamphamvu mpaka kukhuta. Maŵa lidzakhala ngati leroli, mwina mwake nkudzaposa lero limene.’ ” Anthu a Mulungu okhulupirira amafa, ndipo palibe amene amasamalako. Anthu okhulupirika amatengedwa, ndipo palibe amene amamvetsa chifukwa chake. Anthu olungama amachotsedwa, kuti tsoka lisaŵagwere, ndipo amafa mwamtendere. Amene ali olungama amapumula bwino pogona pao. Senderani kuno, inu anthu ochita zoipa, pakuti muli ngati zidzukulu zam'chigololo, zochokera m'zadama. Kodi inu mukuseŵera ndi yani? Kodi mukunena yani? Mukunyoza yani? Kodi ochimwa sindinu? Onyenga sindinu? Mumapembedza mafano pa mitengo ya thundu, patsinde pa mtengo wogudira uliwonse. Mumapereka ana anu ngati nsembe m'zigwa, m'ming'alu yam'mathanthwe. Mumatenga miyala yosalala kumadamboko, ndi kumaipembedza ngati milungu. Mumapereka chopereka cha chakumwa kwa iyo, ndi kuperekanso chopereka cha chakudya. Kodi zimenezi zingandikondweretse? Pa phiri lalitali ndi looneka kutali mudakaika bedi kukachita zadama, komwekonso mudakapereka nsembe. M'nyumba mwanu mwaika mafano ku chitseko ndiponso pa mphuthu. Ine mwandisiya, mwavula zovala zanu, mwakwera pa bedi lanu lalikulu ndi zibwenzi zanu zimene mwazilipira kuti mugone nazo. Kumeneko mwakwaniritsa zilakolako zanu zoipa. Mudadzola mafuta ndi zonunkhira zochuluka, ndipo mudapita kukapembedza fano lija la Moleki. Mudachita kutuma nthumwi kutali, mudazituma ngakhale kumanda komwe. Mudatopa nawo mtunda wouyenda, koma osanena kuti, “Ndingoleka!” Mudapezera zina mphamvu, mwakuti simudalefuke konse. “Kodi ndi milungu yanji imene mudaiwona nkuchita nayo mantha, kotero kuti mudandinamiza nkundiiŵaliratu, osalabada konse za Ine? Kodi mwaleka kundiwopa chifukwa choti ndakhala chete pa nthaŵi yaitali? Mukuganiza kuti zimene mumachita nzolungama, koma makhalidwe anu ndidzaŵaonetsa poyera, ndipo mafano sadzakuthandizani. Mukamafuula kufuna chithandizo, mafano anuwo akupulumutseni! Mphepo idzaiyalula milunguyo, mpweya udzaiwulutsa. Koma amene amakhulupirira Ine, adzalandira dziko lokhalamo, ndi kumapembedza pa phiri langa loyera.” Padzamveka mau akuti, “Lambulani, lambulani ndi kukonza mseu. Chotsani chitsa chilichonse pa njira yodzeramo anthu anga.” Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthaŵi zonse, ndipo dzina lake ndi Woyera uja, akunena kuti, “Ndimakhala pa malo aulemu, oyera. Koma ndimakhalanso ndi anthu odzichepetsa ndi olapa mu mtima, kuti odzichepetsawo ndiŵachotse mantha, olapawo ndiŵalimbitse mtima. “Ndine amene ndidalenga anthu anga ndi kuŵapatsa mpweya wa moyo, motero sindidzapitirira kukangana nawo kapena kuŵakwiyira mpaka muyaya. “Ndidaŵakwiyira chifukwa anali okonda chuma dziŵi. Tsono ndidaŵalanga, ndi kuŵafulatira mokwiya. Koma iwowo adakhalabe ouma mitu, ndipo adapitirira kuchita ntchito zao zoipa. “Ndidaona m'mene ankachitira, komabe ndidzaŵachiritsa. Ndidzaŵatsogolera ndi kuŵatonthoza. Anthu olira nao adzandiyamika ndi milomo yao. Anthu onse akutali ndi apafupi, ndidzaŵapatsa mtendere. Ndidzachiritsa anthu anga. Koma anthu oipa ali ngati nyanja yoŵinduka, yosatha kukhala bata, ndipo mafunde ake amangoponya matope ndi ndere. Palibe mtendere kwa oipa,” akutero Mulungu wanga. Chauta akunena kuti, “Fuula kwambiri, usaleke, mau ako amveke ngati lipenga. Uŵauze anthu anga za kulakwa kwao, uŵauze a m'fuko la Yakobe za machimo ao. Masiku onse iwo amaoneka ngati akufuna kuchita zimene Ine ndifuna. Amangonena kuti afuna kumvera malamulo a Mulungu wao. Amandipempha kuti ndigamule mlandu wao mwachilungamo, ndipo amakondwera kukhala pafupi ndi Mulungu wao.” Anthu akufunsa kuti, “Kodi tizisaliranji zakudya, pamene Inu Chauta simulabadako? Kodi tivutikirenji nkudzichepetsa, pamene Inu simusamalako?” Chauta akunena kuti, “Kunena zoona, tsiku limene mumasala zakudya lija, mumafunafuna zimene zingakupatseni phindu, mumazunza antchito anu onse. Mumati uku mukusala zakudya, uku mukukangana ndi kumenyana, mpaka kutchayana ndi nkhonya zopwetekana. Kodi mukuyesa kuti Ine nkumvera mapemphero anu, chifukwa cha kusala zakudya kotereku. Kodi kusala kumene ndimafuna Ine nkumeneku, kungokhala tsiku loti munthu adzichepetse basi? Inu mumaŵerama pansi ngati udzu, mumayala ziguduli nkuthirapo phulusa kuti mugonepo. Kodi ndiye mumati kusala kumeneku, tsiku lokondwetsa Chauta? “Kusala koona kumene ndimafuna ndi uku: masulani maunyolo ozunzira anzanu, masulani nsinga za goli la kuweruza mokondera. Opsinjidwa muŵapatse ufulu, muthetse ukapolo uliwonse. Anthu anjala muziŵagaŵirako chakudya chanu, osoŵa pokhala muziŵapatsako malo. Mukaona wausiŵa, mpatseni chovala, musalephere kuthandiza amene ali abale anu. “Mukatero, mudzaŵala ngati mbandakucha, ndipo mabala anu adzapola msanga. Ine, kulungama kwanu, ndidzakutsogolerani, ndipo ulemerero wanga udzakutchinjirizani kumbuyo kwanu. “Mukamapemphera ndidzakumverani, ndipo mukandiitana ndidzakuyankhani. Mukaleka kuzunza anzanu, mukasiya kulozana chala, mukaleka kunena zoipa za anzanu, mukamadyetsa anthu anjala, ndi kuthandiza anthu ozunzika, ndiye kuti mdima wokuzingani udzasanduka kuŵala ngati kwa usana. Tsono ndidzakutsogolerani nthaŵi zonse, ndi kukupatsani zabwino. Matupi anu ndidzaŵalimbitsa. Mudzakhala ngati dimba la madzi ambiri, ngati kasupe wa madzi amene saaphwa. Anthu anu adzamanganso nyumba zimene zakhala mabwinja nthaŵi yaitali. Adzamanganso pa maziko akalekale. Apo mudzatchedwa anthu okonza makoma, omanganso nyumba zamabwinja, kuti anthu azikhalamo.” Chauta akunena kuti, “Muzidziletsa kuchita zanuzanu pa Sabata, osagwira ntchito zanu pa tsiku langa loyera. Tsiku la Sabatali muzilitcha kuti chinthu chosangalatsa, tsiku loyera la Chauta muzilitcha kuti chinthu cholemekezeka. Muzililemekeza pakusayendayenda, poleka kugwira ntchito zanu ndiponso posakamba nkhani zachabe. Mukatero ndiye kuti mudzakondwa mwa Ine, Chauta, ndipo ndidzakukwezani ndi kukupambanitsani pa dziko lonse lapansi. Mudzadyerera dziko limene ndidapatsa Yakobe kholo lanu. Ine Chauta ndalankhula zimenezi ndi pakamwa panga.” Chauta si wosoŵa mphamvu, kuti angalephere kukupulumutsani, ndipo si gonthi, kuti nkupanda kumva zimene mukupempha. Machimo anu adakulekanitsani ndi Mulungu wanu, ndipo Iye wakufulatirani chifukwa cha machimo anuwo. Choncho saamva zimene inu mumanena. Manja anu ali psuu ndi magazi a anthu amene mudapha. Mudadziipitsa ndi machimo anu ambiri. Pakamwa panu palankhula zabodza, pamanena zoipa. Palibe amene amaimba mnzake mlandu molungama, palibe wopita ku bwalo lamilandu moona. Amadalira zopanda pake, amangonena mabodza. Amangolingalira zamphulupulu, nachitadi zoipa zimene akuganiza. Ziwembu zao nzoopsa ngati mazira a mphiri, komanso nzosalimba konse ngati ukonde wa kangaude. Wodya mazira a mphiri amafa. Likasweka dzira limodzi mumatuluka mphiri. Ukonde wa kangaude sangauvale ngati nsalu, chimene anthu amapangacho sangafunde konse. Ntchito zao nzoipa ndipo amakonda kuchita zandeu ndi manja ao. Amathamangira kukachita zoipa, sachedwa kupha anthu osalakwa. Maganizo ao onse ali pa zoipa. Kulikonse kumene amapita amasiyako bwinja, ndiponso amaononga. Kumene kuli iwowo, anthu sapeza mtendere. Zonse zimene amachita nzopanda chilungamo. Amayenda m'njira zokhotakhota, ndipo aliyense woyenda m'njira zimenezo sadzapeza mtendere. Anthu akuti, “Chifukwa cha zonsezo chilungamo chatikhalira kutali, ndipo kukhala aungwiro nkosatheka. Timafunafuna kuŵala, koma timangopeza mdima. Timayembekeza kuti kudzakhala mbee, koma kuli bii. Timapapasapapasa ngati anthu akhungu, tili ngati anthu opanda maso. Timaphunthwa masana ngati usiku. Ndife amoyo ndithu, komabe tili ngati anthu akufa. Tonse timabangula ngati zimbalangondo, ndipo timalira modandaula ngati nkhunda. Timayembekeza kuweruza kolungama, koma sitikupeza. Timadikiranso chipulumutso, koma chili nafe kutali. Inu Chauta, takuchimwirani kwambiri. Machimo athu akutitsutsa, zolakwa zathu zili pa ife, ndipo sitingakanepo nchimodzi chomwe. Takupandukirani, takukanani, Inu Chauta, ndipo takana kukutsatani. Tapanikiza anzathu, takupandukirani Inu. Maganizo athu ndi abodza, mau athu ndi onama. Kuweruza kolungama kwalekeka, ndipo kuchita zaungwiro kwaiŵalika. Zoona sizikupezekanso m'mabwalo a milandu, ndipo chilungamo sichikutha kupezeka kumeneko. Zoona zikusoŵa kumeneko, ndipo wina aliyense akapanda kuchita nawo zoipa, amapeza mavuto.” Chauta adaziwona zimenezi ndipo zidamunyansa kuti palibe chilungamo. Chauta adaona kuti palibe munthu ndi mmodzi yemwe adadabwa kuti palibe wochitapo kanthu. Tsono adapambana ndi mphamvu zakezake, ndipo adadzilimbitsa ndi kulungama kwake. Adavala chilungamo ngati chovala chachitsulo chapachifuwa, ndipo kumutu kwake adavala chisoti chachipulumutso. Adavala kulipsira ngati mkanjo, ndipo mkwiyo udakhala ngati chofunda chake, Chauta adzalanga adani a anthu ake molingana ndi zochita zao: adzaonetsa ukali kwa omuukira, ndipo adzalipsira adani ake. Adzalanga ngakhale okhala m'maiko akutali. Motero anthu adzaopa Chauta kuyambira kuvuma mpaka kuzambwe. Iyeyo adzabwera ngati mtsinje waliŵiro, wokankhidwa ndi mphepo yamkuntho. Chauta akuuza anthu ake kuti, “Ndidzabwera ku Yerusalemu kudzapulumutsa a fuko la Yakobe amene adaleka machimo ao. “Ndipo ndidzapangana nawo chipangano chakuti, ‘Kuyambira tsopano mpaka muyaya, mzimu wanga umene uli pa iwe, ndiponso mau anga amene ndidaika m'kamwa mwako, sizidzachokeranso m'kamwa mwako kapena m'kamwa mwa ana ako kapena mwa adzukulu ako mpakampaka.’ ” Iwe Yerusalemu dzuka, ŵala, kuŵala kwako kwayamba. Ulemerero wa Chauta wakuŵalira. Mdima udzaphimba dziko lapansi, mdima wandiweyani udzagwa pa anthu a mitundu ina. Koma iwe, Chauta adzakuŵalira, ulemerero wake udzaoneka pa iwe. Anthu a mitundu ina adzatsata kuŵala kwako, mafumu adzalondola kunyezimira kwako konga dzuŵa limene likutuluka kumene. Yang'ana pozungulira, uwone zimene zikuchitika. Onse akusonkhana kuti abwere kwa iwe. Ana ako aamuna adzabwera kuchokera kutali. Ana ako aakazi adzatengedwa m'manja ngati ana. Udzaona zimenezi, ndipo udzakondwa, mtima wako udzalumpha ndi chimwemwe. Chuma chakunyanja chidzabwera kwa iwe. Chuma cha maiko onse chidzabwera kwa iwe. Kudzafika mtindiri wa ngamira, ngamira zing'onozing'ono, kuchokera ku Midiyani ndi ku Efa. Onse a ku Sheba adzabwera. Adzakhala atatenga golide ndi lubani, ndipo adzatamanda Chauta mokweza mau. Ziŵeto zonse za ku Kedara adzazisonkhanitsa kwanu, nkhosa zamphongo za ku Nabayoti zidzakuthandizani pamene mudzazisoŵa. Zidzaperekedwadi pa guwa ngati nsembe. Choncho Ine Chauta ndidzapatsa Nyumba yanga ulemerero waukulu kupambana kale. Kodi nzinthu zanji zikuti yakaliyakali ngati mitambozi, zikuchita ngati nkhunda zobwerera kumakomo kwakezi? Zimenezo ndi zombo zochokera ku maiko akutali, za ku Tarisisi zili patsogolo. Zikudzatula ana anu amene atenga siliva ndi golide, kuti alemekeze dzina la Chauta, Mulungu wanu, Woyera uja wa Israele, chifukwa Iyeyo adakupatsani ulemerero. Chauta akuuza Yerusalemu kuti, “Alendo adzamanganso malinga ako, ndipo mafumu ao adzakutumikira. Ndidakulanga pamene ndinali wokwiya, koma tsopano ndidzakukomera mtima ndi kukuchitira chifundo. Zipata zako zidzakhala zotsekula nthaŵi zonse. Usana ndi usiku womwe sadzazitseka, kuti choncho anthu a mitundu yonse adzabwere ndi chuma chao kwa iwe, akuyenda pa mdipiti, mafumu ao ali patsogolo. Koma maiko ndi mafumu amene sakutumikira, adzaonongekeratu. Anthu a mitundu imeneyo adzaonongeka kotheratu.” “Mitundu itatu ija ya mitengo ya paini, imene ili yabwino kwambiri m'nkhalango ya ku Lebanoni, adzabwera nayo kuti akongoletsere Nyumba yanga. Motero m'Nyumba m'mene ndimakhala Ine mudzalemekezeka. Ana a amene adaakuzunzapo adzabwera ndipo adzakugwadira kuwonetsa ulemu. Onse amene adaakunyozapo adzakuŵeramira mpaka pansi. Adzakutchula kuti Mzinda wa Chauta, ndiye kuti Ziyoni, mzinda wa Woyera uja wa Israele.” “Ngakhale anthu adakusiya nadana nawe, osadutsanso mwa iwe, ndidzakukuza mpaka muyaya, ndipo udzakhala malo a chimwemwe pa mibadwo ndi mibadwo. Monga mwana woyamwa udzadya chuma cha anthu a mitundu ina, ndipo mafumu ao omwe adzakusamala. Motero udzadziŵa kuti Ine Chauta ndine Mpulumutsi wako, ndipo kuti ndine Momboli wako, Wamphamvu uja wa Yakobe.” “Ndidzakupatsa golide m'malo mwa mkuŵa, m'malo mwa chitsulo ndidzakupatsa siliva, mkuŵa m'malo mwa mtengo, chitsulo m'malo mwa mwala. Okuyang'anira ndidzaŵasandutsa amtendere, okulamulira ndidzaŵasandutsa olungama. Ziwawa sizidzamvekanso. Dziko lako silidzaonongekanso. Ndidzakhala ngati linga lokuteteza, ndipo udzanditamanda chifukwa chokupulumutsa.” “Sipadzafikanso dzuŵa loti likuŵalire masana, kapena mwezi wokuŵalira usiku. Koma Ine Chauta ndiye ndidzakuŵalire mpaka muyaya. Ine Mulungu wako ndiye ndidzakhale ulemerero wako. Chokuunikira ngati dzuŵa sichidzaloŵanso, ndipo chokuunikira ngati mwezi sichidzazimiriranso, chifukwa ndi Chauta amene adzakhala kuŵala kwako mpaka muyaya. Choncho masiku ako olira adzatha. Anthu ako onse adzayenda m'njira zoyenera, ndipo dzikolo lidzakhala lao mpaka muyaya. Anthuwo ndidaŵaika ndine, ndidaŵalenga ndine, kuti aonetse ulemerero wanga kwa onse. Ngakhale kabanja kakang'onong'ono kadzasanduka fuko, ndipo kafuko kakang'onong'ono kadzasanduka mtundu wamphamvu. Ndidzachita zimenezi mofulumira nthaŵi yake itafika. Ine ndine Chauta.” Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula. Wandituma kukalengeza za nthaŵi imene Chauta adzapulumutsa anthu ake ndi kulipsira adani ake. Wanditumanso kukatonthoza olira. Wandituma kuti ndiŵakonzere zofunika olira a ku Ziyoni, ndiye kuti ndiŵapatse maluŵa achisangalalo m'malo mwa phulusa lachisoni, ndiŵapatse mafuta osonyeza kukondwa m'malo mwa kulira, ndiŵapatse chovala cha chikondwerero m'malo mwa kutaya mtima. Tsono adzatchedwa mitengo yamphamvu yachilungamo, yoibzala Chauta, kuti Iye mwini apezepo ulemu. Adzamanganso mabwinja akale a mzinda, adzautsa nyumba zimene zidaaonongeka. Adzakonzanso mizinda imene idaapasuka, ndiponso malo osiyidwa chiyambire cha kalekale. “Anthu achilendo adzakutumikirani, ndipo adzaŵeta ziŵeto zanu, iwo omwewo adzalima minda yanu, makamaka minda yanu yamphesa. Koma inu mudzatchedwa ansembe a Chauta, ponena za inu anthu adzati ndinu atumiki a Mulungu. Mudzadyerera chuma cha anthu a mitundu ina, ndipo mudzanyadira ulemu umene mwaŵalanda. Popeza kuti mudalandira manyazi, manyozo ndi zotukwana moŵirikiza, tsopano mudzalandira chigawo cha dziko lanu moŵirikizanso. Chimwemwe chanu chidzakhala chamuyaya.” “Ine Chauta ndimakonda chilungamo, ndimadana ndi zakuba ndi zoipa. Anthu anga ndidzaŵapatsa mphotho mokhulupirika, ndidzapangana nawo chipangano chosatha. Ana ao adzakhala odziŵika pakati pa anthu a mitundu ina, zidzukulu zaonso zidzakhala zotchuka pakati pa anthu onse. Aliyense woŵaona adzazindikira kuti ndi anthu amene Ine Chauta ndidaŵadalitsa.” Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta, mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso. Wandiveka mkanjo wa chilungamo. Zinali ngati mkwati wamwamuna wavala nkhata ya maluŵa m'khosi, ndiponso ngati mkwati wamkazi wavala mikanda ya mtengo wapatali. Monga momwe nthaka imameretsera mbeu, ndiponso monga momwe munda umakulitsira zimene adabzalamo, momwemonso Chauta adzaonetsa chilungamo ndi ulemerero wake pamaso pa anthu onse. Chifukwa chokonda Ziyoni sindidzakhala chete, chifukwa chokonda Yerusalemu sindidzakhala chete, mpaka chilungamo chake chitaoneka poyera ngati kuŵala, ndipo chipulumutso chake chitaoneka ngati muuni woyaka. Iwe Yerusalemu, mitundu ya anthu idzakuwona utapambana pa nkhondo, mafumu ao onse adzaona ulemerero wako. Adzakuitanira dzina latsopano, limene adzakutche ndi Chauta yemwe. Udzakhala ngati chisoti chaufumu chokongola m'manja mwa Chauta, ngati nsangamutu yaulemerero m'manja mwa Mulungu wako. Sudzatchedwanso “Wosiyidwa,” dziko lako silidzatchedwanso “Chipululu.” Dzina lako latsopanolo lidzakhala “Ndikukondwera naye.” Dziko lako lidzatchedwa “Wokwatiwa mwachimwemwe,” chifukwa choti Chauta akukondwera nawe, ndipo adzakhala ngati mwamuna wa dziko lako. Monga mnyamata amakwatira namwali, chonchonso mmisiri wodzakumanganso adzakukwatira. Monganso mkwati wamwamuna amakondwerera mkwati wamkazi, chonchonso Mulungu adzasangalala nawe. Iwe Yerusalemu, pa malinga ako ndaikapo alonda, usana wonse ndi usiku wonse sadzakhala chete. Inu amene mumakumbutsa Chauta za malonjezo ake, musapumule. Musaleke kumkumbutsa mpaka atakhazikitsanso Yerusalemu, ndi kuusandutsa mzinda umene dziko lapansi lidzautamanda. Chauta adalumbira motsimikiza, ndipo adzasunga malumbirowo ndi mphamvu zake. Adati, “Adani ako sadzadyanso tirigu wako, ndipo alendo sadzamwanso vinyo wako. Koma inu amene mudabzala ndi kukolola tiriguyo, ndiye amene mudzadye buledi, ndipo mudzatamanda Chauta. Inu amene munkasamala mitengo yamphesa ndi kumathyola mphesa, ndiye amene mudzamwe vinyo m'mabwalo a Nyumba yanga.” Tulukani, inu a mu Yerusalemu, inde tulukani mumzindamo, mukakonze mseu woti anthu anu obwerera kwao aziyendamo. Mulambule mseu waukulu, ndipo muchotsemo miyala. Mukweze mbendera kuti mitundu ya anthu iziwona. Chauta walengeza ku dziko lonse lapansi zakuti muuze anthu a ku Yerusalemu kuti, “Chipulumutso chanu chikubwera. Chauta akubwera ndi mphotho yake, akubwera nazo zokuyenererani. Mudzatchedwa anthu opatulika a Mulungu, anthu amene Chauta waŵapulumutsa. Iwe Yerusalemu, udzatchedwa Mzinda wokondedwa wa Chauta, mzinda umene Mulungu sadausiye.” “Ndaninso kodi akuchokera ku Edomuyu, atavala zofiira za ku Bozira? Ndani ameneyu wovala zovala zokongola, akuyenda monyadira mphamvu zake? Ndi Ineyo, wolankhula zachilungamo, ndiponso wa mphamvu zoti nkupulumutsa.” Nanga bwanji zovala zanu zili psuu, ndiponso zikuwoneka ngati za munthu woponda mphesa? “Ndapondereza ndekha anthu a mitundu ina ngati mphesa, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adadzandithandiza. Ndidaŵapondereza ndili wokwiya, magazi ao nkufalikira pa zovala zanga. Mumtima mwanga ndidatsimikiza kuti lafika tsiku loti ndilange adani anga molipsira, chafika chaka choti ndipulumutse anthu anga. Ndidayang'ana, koma panalibe wondithandiza. Ndidadabwa kwabasi kuti panalibe wondichirikiza. Choncho ndidapambana ndi mphamvu za ine ndekha, unkandilimbitsa ndi mkwiyo wanga. Ndidapondereza anthu a mitundu ina ndili wokwiya, ndipo ndidaŵasakaza. Magazi ao ndidaŵathira pansi.” Ndidzasimba za chikondi chosasinthika cha Chauta. Ndidzamtamanda chifukwa cha zonse zimene watichitira. Wadalitsa kwambiri anthu a ku Israele, potsata chifundo ndi kukula kwa chikondi chake chosasinthika. Chauta adati, “Iwo ndi anthu anga, ana anga amene sadzandinyenga.” Motero adaŵapulumutsa. Adavutika poona mavuto ao onse, Mngelo wochokera kwa Iye adaŵapulumutsa. Adaŵaombola mwa chikondi ndi chifundo chake. Wakhala akuŵasamala ngati ana kuyambira kale. Komabe iwo adampandukira, namkwiyitsa Mulungu. Motero Chauta adasanduka mdani wao, ndipo adamenyana nawo nkhondo. Pamenepo anthuwo adakumbuka zamakedzana, masiku a Mose mtumiki wake, ndipo adafunsa kuti, “Ali kuti tsopano Chautayo amene adapulumutsa anthu ake pamodzi ndi mtsogoleri wao pa nyanja? Ali kuti Chautayo amene adaika mwa anthu ake mzimu wake woyera? Ali kuti Chautayo amene adachita zinthu zodabwitsa ndi mphamvu zake zazikulu kudzera mwa Mose? Adagaŵa madzi am'nyanja, anthu ake akuwona, kuti dzina lake limveke mpaka muyaya. Adaŵayendetsa pa nyanja pouma, ndipo monga kavalo woyenda m'chipululu, iwo sadakhumudwe. Mzimu wa Chauta udaŵapumitsa, monga m'mene ng'ombe zimapumulira ku dambo.” Motero Inu Chauta mudatsogolera anthu anu, kuti dzina lanu lilemekezeke. Inu Chauta kumwambako, ku malo anu oyera ndi aulemerero, mutiyang'ane ife. Kodi chisamaliro chanu chili kuti? Mphamvu zanu zili kuti? Simukutiwonetsanso chikondi chanu ndi chifundo chanu. Inu ndinu Atate athu ndithu, ngakhale Abrahamu satidziŵa, ngakhale Israele sakutivomera. Koma Inu, Chauta, ndinu Atate athu, ndinu Momboli wathu kuyambira kalekale. Chifukwa chiyani mukutisokeretsa pa njira zanu? Bwanji mukutilola kuti tizikhala ouma mtima kotero kuti sitikukuwopaninso? Bwererani chifukwa cha atumiki anu, mafuko a anthu amene ali choloŵa chanu. Anthu anu opatulika adangoti atakhala nawo malo anu oyera kanthaŵi pang'ono, adani adaŵasakaza malowo. Tasanduka ngati anthu amene simudatilamulepo, ngati kuti sitidakhalepo anthu anu. Inu Chauta, bwanji osang'amba mlengalenga kuti mutsike pansi? Bwanji osati mapiri agwedezeke poona Inu, monga momwe moto umatenthera tchire, ndiponso monga momwe umagadutsira madzi, kuti adani anu akudziŵeni, ndipo kuti anthu a mitundu ina anjenjemere pamaso panu. Nthaŵi ina yake mudatsika pansi pano kudzachita zinthu zoopsa zimene sitidaziyembekeze. Mapiri atakuwonani, adanjenjemera ndi mantha. Chikhalire palibe ndi mmodzi yemwe amene adaona kapena kumva za Mulungu wina wonga Inu, wochitira zotere anthu omkhulupirira. Inu mumaŵalandira onse amene amakondwera pochita zolungama, amene amayesetsa kuyenda monga Inu mufunira. Inde mudatikwiyira, komabe ife tidapitiriza kuchimwa. Takhala ochimwadi nthaŵi yaitali, kodi tidzapulumuka kumene? Tonsefe tasanduka ngati anthu oipitsidwa, ndipo ntchito zathu zonse zabwino zakhala ngati nsanza zauve. Tonsefe tikufota ngati masamba, tikuuluzika ndi machimo athu, ngati tikuuluzika ndi mphepo. Palibe amene amatamira dzina lanu popemphera, kapena amene amatekeseka nzopempha chithandizo kwa Inu. Mwatifulatira ndipo mwatisandutsa akapolo a machimo athu. Komabe Inu Chauta, ndinu Atate athu. Ife tili ngati mtapo, Inu muli ngati woumba. Mudatipanga tonse ndi manja anu. Motero musatikwiyire kopitirira, ndipo musakumbukire machimo athu mpaka muyaya. Tapota nanu mutiganizireko, tonsefetu ndife anthu anu. Mizinda yanu yoyera yasanduka chipululu, Ziyoni wasanduka thengo, Yerusalemu wasanduka wamasiye. Nyumba yathu yoyera ndi yokongola, m'mene makolo athu ankakutamandirani, yapsa ndi moto. Malo onse amene tinkaŵakonda asanduka bwinja. Kodi Inu Chauta, simukuvutika nazo zimenezi? Monga mudzangokhala chete nkumatizunza mwankhanza? Chauta adati, “Ndinali wokonzeka kumva mapemphero a anthu amene sadandipemphere. Ndinali wokonzeka kuti andipeze anthu amene sadandifunefune. Mtunduwo sudapemphere kwa Ine ngakhale nthaŵi zonse ndinali wokonzeka kuŵayankha kuti, ‘Ine ndili pano, ndikuthandizani.’ Nthaŵi zonse ndakhala wokonzeka kuŵalandira mwaufulu anthu ondipandukiraŵa, amene amachita zoipa namatsata njira zao chifukwa cha kuuma mitu kwao. Amandikwiyitsa mopanda manyazi. Amapereka nsembe zachikunja m'minda, ndipo amafukiza lubani pa maguwa anjerwa achikunja. Amakatandala ku manda, amachezera kumalo obisika usiku. Amadya nyama yankhumba, namamwa msuzi wa nyama zoperekera nsembe zachikunja. “Amauza ena kuti, ‘Khalani panokha, osatiyandikira, chifukwa ndife opatulika.’ Sindingathe kupirira nawo anthu otere. Ukali wanga pa iwo uli ngati moto wosazima. Ndatsimikiza kale za chilango chao, ndipo mlandu wao ndaulemba kale. Ndidzaŵalanga chifukwa cha machimo ao. Ndidzaŵalanganso chifukwa cha machimo a makolo ao. Iwowo afukiza lubani pa mapiri a mafano achikunja, ndipo andinyoza Ine pa zitunda zao. Nchifukwa chake ndidzaŵalanga potsata zimene achita.” Chauta akuti, “Pamene madzi adakalimo m'mphesa, anthu amati, ‘Musaziwononge, zokoma zidakalimo.’ Inenso ndidzaŵatero anthu anga, sindidzaŵaononga onse. M'banja la Yakobe ndidzatulutsamo zidzukulu, ndipo a m'banja la Yuda adzalandira dziko langa lamapiri ngati choloŵa chao. Anthu anga osankhidwa adzalilandiradi, atumiki anga adzakhala kumeneko. Chigwa cha Saroni chidzakhala busa la nkhosa, ndipo Chigwa cha Akori chidzasanduka malo ousirapo msambi wa ng'ombe, kwa anthu anga ondifunafuna Ine. Koma inu amene mumakana Chauta, amene mumaiŵala phiri langa lopatulika, amene mumapembedza Gadi ndi Meni, milungu yobweretsa mwai ndi tsoka, nonsenu ndidzakufetsani ku nkhondo. Nonsenu mudzaphedwadi, chifukwa simudayankhe m'mene ndidakuitanani, ndipo simudamve m'mene ndidalankhula, koma mudachita zoipa pamaso panga. Mudasankha kuchita zoipa m'malo mwa zabwino.” Nchifukwa chake Chauta akunena kuti, “Atumiki anga adzadya, koma inu mudzakhala ndi njala, atumiki anga adzamwa, koma inu mudzakhala ndi ludzu. Atumiki anga adzakondwa, koma inu mudzakhala ndi manyazi. Iwo adzaimba mokondwa, koma inu mudzalira kwambiri chifukwa chovutika mu mtima. Mudzalira mofuula chifukwa cha kumva kuŵaŵa mu mtima. Anthu anga osankhidwa adzatchula dzina lanu potemberera, ndipo Ine Chauta ndidzakuphani. Koma amene amandimvera ndidzaŵapatsa dzina lina latsopano. Motero wopempha madalitso m'dzikomo, adzachita zimenezo kwa Mulungu wolankhula zoona. Ndipo wochita malumbiro m'dzikomo, adzalumbira m'dzina la Mulungu wolankhula zoona, chifukwa choti mavuto akale aiŵalika ndipo achotsedwa pamaso panga.” Chauta akunena kuti, “Ndikulenga thambo lam'mwamba latsopano ndi dziko lapansi latsopano. Zakale sadzazikumbukiranso, zidzaiŵalika kotheratu. Koma inu mukhale osangalala ndi okondwa mpaka muyaya, chifukwa cha zimene ndidzalenga. Ndidzalengadi Yerusalemu watsopano wodzaza ndi chimwemwe, ndipo anthu ake adzakhala okondwa. Mwiniwakene ndidzakhala wokondwa kwambiri chifukwa cha Yerusalemu, ndipo ndidzasangalala chifukwa cha anthu ake. Kumeneko sikudzamvekanso kulira kapena kudandaula. Ana sadzafanso ali akhanda, ndipo nkhalamba zonse zidzakwaniritsa zaka zao zonse. Amene adzafe ali a zaka zana limodzi zokha adzaoneka ngati anyamata. Kufa zisanakwane zaka zana limodzi kudzasonyeza kutembereredwa. Anthu adzamanga nyumba ndi kukhalamo. Adzabzala mipesa, ndipo adzadyerera zipatso zake. Sadzamanga nyumbazo kuti anthu ena azikhalamo, ndipo sadzabzala mipesayo kuti anthu ena azidyerera zipatso zake. Anthu anga adzakhala ndi moyo wautali ngati mitengo. Ndipo anthu anga osankhidwa adzakondwerera ntchito za manja ao nthaŵi yaitali. Sadzagwira ntchito pachabe, kapena kubereka ana kuti aone tsoka, chifukwa adzakhala anthu odalitsidwa ndi Chauta, iwowo ndi zidzukulu zao zomwe. Ndidzaŵayankha asanatsirize nkomwe kupemphera, ndidzaŵamva akulankhula kumene. Mimbulu ndi anaankhosa zidzadyera pamodzi. Mkango udzadya udzu monga ng'ombe. Fumbi ndiye lidzakhale chakudya cha njoka. Pa phiri langa loyera la Ziyoni sipadzakhala chinthu chopweteka kapena choononga,” akuterotu Chauta. Chauta akunena kuti, “Thambo lam'mwamba ndiye mpando wanga waufumu, dziko lapansi ndiye chopondapo mapazi anga. Kodi ndi nyumba yotani imene mungathe kundimangira inu? Ndi malo otani amene inu mungandikonzere kuti Ine ndizipumulirapo? Zinthu zonsezi ndidazilenga ndine, tsono zonsezi nzanga,” akutero Chauta. “Anthu amene ndimakondwera nawo ndi aŵa: odzichepetsa ndi olapa, ondiwopa ndi omvera mau anga. “Koma pali ena amene amangochita zoŵakomera. Kwa iwo nchimodzimodzi kupereka ng'ombe yamphongo ngati nsembe kapena kupha munthu, kupha mwanawankhosa kuti aperekere nsembe kapena kupha galu, kupereka chopereka cha chakudya kapena kupereka magazi a nkhumba, kupereka lubani ku nsembe yachikumbutso kapena kupembedza fano. Anthu ameneŵa mtima wao umakondwera nazo zonyansa zao. Ine tsono ndidzaŵagwetsera chilango ndipo ndidzaŵachititsa mantha, chifukwa nditaŵaitana, palibe amene adandiyankha, kapena kutchera khutu pamene ndinkalankhula. Adachita zoipa pamaso panga, adasankhula kuchita zimene zimandinyansa.” Imvani mau a Chauta, inu amene mumanjenjemera akamalankhula. Iye akuti, “Abale anu omwe amene amadana nanu nakukanani chifukwa cha dzina langa, amati, ‘Chauta alemekezeke, kuti ife tiwone chimwemwe chanu.’ Koma ndi iwowo amene adzachite manyazi. “Imvani mfuu mu mzinda! Imvani liwu m'Nyumba ya Mulungu, liwu la Chauta amene akulanga adani ake. “Mzinda wangawu uli ngati mai amene akubadwitsa mwana asanayambe kumva zoŵaŵa zake, amene akubala mwana wamwamuna kupweteka kusanayambike. Ndani adamvapo zoterezi? Ndani adaziwonapo zoterezi? Kodi dziko nkupangika tsiku limodzi? Kodi mtundu wa anthu nkubadwa tsiku limodzi? Koma Ziyoni adabala ana ake aamuna, atangoyamba kuvutika kumene. Kodi ine ndidzafikitsa anthu anga mpaka nthaŵi yobala, koma osalola kuti abaledi?” Akuterotu Chauta. “Kodi Ine, amene ndili wobalitsa, ndingatseke mimba nthaŵi imeneyo?” Akuterotu Mulungu wako. “Kondwera nayeni Yerusalemu, musangalale chifukwa cha iye, inu nonse amene mumakonda mzinda umenewu. Kondwera nayeni mwachimwemwe, nonsenu amene mukumlira. Mudzalandira chitonthozo ndi kukondwera nacho kwambiri. Mudzagaŵana naye ulemerero wake ndi kusangalala nawo.” Chauta akunena kuti, “Ndidzakupatsa zabwino zochuluka ngati mtsinje wa madzi. Chuma cha mitundu ya anthu chidzafika kwa inu ngati mtsinje wosefukira. Mudzakhala ngati mwana woyamwa amene mai wake wamnyamulira pambalipa, kapena akumluluza pa maondo. Ndidzakusangalatsani ku Yerusalemu monga momwe mai amasangalatsira mwana wake. Mudzasangalala poona zimenezi. Zidzakulimbitsani ndi kukupatsani moyo wamphamvu. Tsono mudzadziŵa kuti Ine Chauta ndimathandiza amene amandimvera, ndipo ndimakwiyira adani anga.” “Pajatu Chauta adzabwera ndi moto. Ndipo magaleta ake adzafika ngati mkuntho. Iye adzaonetsa poyera ukali wake, ndipo adzalanga adani ake ndi malaŵi a moto. Adzalanga anthu onse a pa dziko lapansi ndi moto ndi lupanga. Alipo ambiri amene Chauta adzaŵapha.” Chauta akunena kuti, “Amene akuti akudzipatula ndi kudziyeretsa pamene akufuna kuchita miyambo yam'minda ija, ali ndi mtsogoleri wao yemwe, nkumadya nyama yankhumba, mbeŵa ndi zonyansa zina, onsewo adzafera limodzi,” akuterotu Chauta. “Ndikudziŵa ntchito zao ndi maganizo ao. Ndikubwera kudzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse ndi a zilankhulo zonse. Adzabweradi ndipo adzaona ulemerero wanga. “Ndidzaika chizindikiro pakati pao. Mwa iwowo padzakhala ena opulumukako amene ndidzaŵatuma kwa anthu a mitundu ina, monga a ku Tarisisi, a ku Puti ndi a ku Ludi, akatswiri a mauta, ndiponso ku Tubala, ku Yavani, ndi ku maiko akutali amene sadamvepo za mbiri yanga kapena kuwona ulemerero wanga. Iwowo adzalalika za ulemerero wanga pakati pa anthu a mitundu ina. Ndipo adzabwera nawo abale anu onse kuchokera kwa anthu a mitundu yonse, kuti akhale mphatso kwa Ine. Adzabwera nawo ku phiri langa loyera la Yerusalemu, abale anuwo ataŵakweza pa akavalo, abulu, ngamira ndiponso pa magaleta ndi ngolo. Adzabwera nawo monga momwe Aisraele amabwerera ndi zopereka za chakudya ku Nyumba ya Mulungu, atazitenga m'ziŵiya zotsukatsuka, ndipo ena mwa iwo ndidzaŵasandutsa ansembe ndi Alevi,” akutero Chauta. “Monga momwe dziko lapansi latsopano ndi dziko lakumwamba latsopano, zimene ndidzapange, zidzakhala mpaka muyaya pamaso panga, chonchonso zidzukulu zanu ndi dzina lanu zidzakhala mpaka muyaya. Anthu a mitundu yonse adzabwera kudzandipembedza ku Yerusalemu, pa chikondwerero chilichonse cha pokhala mwezi, ndi tsiku la Sabata lililonse,” akutero Chauta. “Akamachoka, adzaona mitembo ya anthu amene adandipandukira. Mphutsi zimene zidzaŵadya sizidzafa, ndipo moto umene udzaŵatentha sudzazima. Anthu a mitundu yonse poŵaona adzanyansidwa nawo.” Aŵa ndi mau a Yeremiya, mwana wa Hilikiya, mmodzi mwa ansembe a ku Anatoti, m'dziko la Benjamini. Chauta adalankhula naye pa nthaŵi ya Yosiya, mfumu ya ku Yuda, mwana wa Amoni, pa chaka cha khumi ndi chitatu cha ufumu wake. Chauta adalankhula nayenso pa nthaŵi ya Yehoyakimu, mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda, mpaka mwezi wachisanu wa chaka cha khumi ndi chimodzi cha Zedekiya, mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda, pamene anthu a ku Yerusalemu adatengedwa ukapolo. Chauta adandiwuza kuti, “Ndisanakulenge m'mimba mwa mai wako, ndinali nditakudziŵa kale. Usanabadwe nkomwe, ndinali ntakupatula kale, ndidakuika kuti ukhale mneneri kwa anthu a mitundu yonse.” Ine ndidati, “Ha, Ambuye Chauta! Ine ndine mwana, kulankhula sindidziŵa.” Koma Iye adandiyankha kuti, “Usati, ‘Ndine mwana.’ Udzapita ndithu kwa anthu onse kumene ndidzakutuma, ndipo chilichonse chimene ndidzakulamula udzachilankhula. Usaŵaope, Ine ndili nawe, ndidzakupulumutsa,” akuterotu Chauta. Tsono Chauta adatambalitsa dzanja lake nakhudza pakamwa panga. Ndipo adandiwuza kuti, “Tamvera, ndikuika mau anga m'kamwa mwako. Ndikukuika lero kuti ukhale ndi ulamuliro pa maiko a anthu ndi maufumu ao, kuti uzule ndi kugwetsa, kuti uwononge ndi kugumula, kuti umange ndi kubzala.” Chauta adandifunsa kuti, “Yeremiya, kodi ukuwona chiyani?” Ine ndidayankha kuti, “Ndikuwona nthambi ya mtowo.” Chauta adati, “Waona bwino. Ineyo ndikuwonetsetsa kuti zichitikedi zimene ndidanena.” Chauta adandifunsa kachiŵiri kuti, “Kodi ukuwona chiyani?” Ine ndidayankha kuti, “Ndikuwona mbiya yogaduka, yafulatira kumpoto.” Apo Iye adandiwuza kuti, “Ndiye kuti tsoka la anthu a m'dziko lino lidzachokera kumpoto. Ndikuitana anthu a mafuko onse a maufumu akumpoto,” akuterotu Chauta. “Mafumu ao adzabwera, aliyense adzaika mpando wake waufumu pa zipata za Yerusalemu, ndiponso pozungulira malinga ake. Iwo adzazinganso mizinda yonse ya Yuda. Ndidzatulutsa mlandu wanga wotsutsa anthu anga, chifukwa cha zoipa zimene adachita pakundisiya Ine. Adafukiza lubani kwa milungu ina, namapembedza zimene adapanga ndi manja ao. Koma iwe Yeremiya, ukonzeke. Nyamuka, ukaŵauze zonse zimene ndikukulamula. Iwowo asakuwopse, kuwopa kuti Ineyo ndingakuwopse iwo akuwona. Lero ine ndikukulimbitsa ngati mzinda wamalinga, mzati wachitsulo, ndiponso ngati makoma amkuŵa, kuti usachite mantha ndi wina aliyense m'dziko lonse, kaya ndi mafumu a ku Yuda, nduna zakumeneko, ansembe kapena anthu wamba. Iwo adzalimbana nawe, koma sadzakupambana, pakuti ine ndili nawe ndipo ndidzakupulumutsa,” akuterotu Chauta. Chauta adandiwuza kuti ndikalengeze kwa anthu a ku Yerusalemu mau ake akuti, “Ndikukumbukira m'mene munkakhulupirikira pa unyamata wanu, m'mene poyamba paja munkandikondera monga amachitira mkwati wamkazi. Mudanditsata m'chipululu, m'dziko losabzalamo kanthu. Iwe Israele udaali wopatulika wa Chauta. Udaali ngati chipatso chake choundukula. Ndidaika zoŵaŵa ndi mavuto aakulu, pa onse amene adakuzunza, ndipo tsoka linkaŵagwera,” akutero Chauta. Inu zidzukulu za Yakobe, mabanja onse a Israele, mverani mau a Chauta. Iye akukufunsani kuti, “Kodi makolo anu adandipeza ncholakwa chanji kuti andithaŵe? Adatsata milungu yachabechabe, iwonso nkusanduka achabechabe. Sadalabadeko za Ine Chauta, ngakhale ndine amene ndidaŵatulutsa m'dziko la Aejipito, ndi kuŵatsogolera m'chipululu, m'dziko louma ndi lokumbikakumbika, m'dziko lachilala ndi la mdima wandiweyani, m'dziko limene munthu sadutsamo, kumene sikukhala munthu konse. Ndidakufikitsani ku dziko lachonde kuti mudye zipatso zake ndi zabwino zake zina. Koma mutangoloŵa m'dzikolo, mudaliipitsa, dziko limene ndidakupatsani mudalisandutsa lonyansa. Nawonso ansembe sadafunse kuti, ‘Chauta ali kuti?’ Akatswiri a malamulo sadandidziŵe. Olamulira adandipandukira. Aneneri ankalosa m'dzina la Baala, ndipo ankatsata milungu yachabechabe. “Tsono ndidzakuimbanibe mlandu,” akuterotu Chauta. “Ndidzaimbanso mlandu zidzukulu zanu. Pitani chakuzambwe, ku chilumba cha Kitimu, mukaone, tumani anthu chakuvuma, ku Kedara, akafufuze. Mudzaona kuti zoterezi sizidachitikepo nkale lonse. Kodi ulipo mtundu wa anthu uliwonse umene udasinthapo milungu yake, ngakhale kuti si milungu konse? Komabe anthu anga asinthitsa Mulungu wao waulemerero ndi milungu yachabechabe. Inu maiko akumwamba, dabwa nazoni zimenezi, njenjemerani ndi mantha, akuterotu Chauta. Anthu anga achita machimo aŵiri: andisiya Ine kasupe wa madzi opatsa moyo, adzikumbira okha zitsime, zitsime zake zong'aluka, zosatha kusunga madzi. “Israele si kapolotu ai, sadabadwire mu ukapolo. Nanga chifukwa chiyani amuwononga chotere? Anthu a mitundu ina ambangulira ndi kumuwopsa ngati mikango. Dziko lake alisandutsa chipululu. Mizinda yake adaiwononga, idasanduka mabwinja. Aejipito a ku Memfisi ndi a ku Tapanesi akuphwanyani mitu. Zimenezi zakuwonekerani chifukwa mudasiya Chauta, Mulungu wanu, pamene Iye adakuikani pa njira yabwino. Nanga tsopano mudzapindulanji mukadzapita ku Ejipito, kukamwa madzi a m'Nailo? Mudzapeza phindu lanji mukadzapita ku Asiriya kukamwa madzi a mu mtsinje wa Yufurate? Mudzalangidwa ndi machimo anu omwe: poti mwandikana, ndidzakuimbani mlandu. Muganizire bwino za kuipa kwake kwa kundisiya Ine, Chauta, Mulungu wanu. Mulingalire kuŵaŵa kwake kwa kukhala osandiwopa,” akuterotu Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse. “Kuyambira masiku amakedzana inu mudathyola goli lanu ndi kudula nsinga zanu. Mudati, ‘Sitidzakutumikirani!’ Ndithu inu mwakhala ngati mkazi wadama, mukupembedza milungu ina pochita zadama pa phiri lililonse ndiponso pansi pa mtengo wogudira uliwonse. Komabe ndidaakuwoka iwe Israele ngati mtengo wa mphesa wosankhidwa, udaali mpesa wabwino kwambiri. Nanga wasanduka bwanji mpesa wachabechabe, wonga wakutchire? Ngakhale usambire soda, ngakhale usambire sopo wambiri, kuthimbirira kwa tchimo lako kumaonekabe pamaso panga,” akuterotu Ambuye Chauta. “Uneneranji kuti, ‘Ine sindidadziipitse, sindidatsate Baala?’ Kumbukira m'mene udachimwira m'chigwamo, zindikira zimene wachita. Wakhala ngati ngamira yaikazi, yothamanga uku ndi uku. Wakhala ngati mbidzi yaikazi yozoloŵera m'chipululu, yonka nipunika pa nthaŵi yake yachisika. Kodi angailetse chilakolako chakecho ndani? Mphongo iliyonse yoikhumba sidzavutika, idzaipeza pa nthaŵi yakeyo. Iwe Israele, lekatu, nsapato zingakuthere ku phazi, kukhosi kwako kungaume ndi ludzu potsatira milungu ina. Koma iwe ukuti, ‘Ai toto, sindingathe kuchitira mwina, ndimakonda milungu yachilendoyi, sindingaleke kuitsata.’ “Banja la Israele lidzachita manyazi, monga momwe mbala imachitira manyazi akaigwira. Aisraele, mafumu ao ndi akalonga ao, ansembe ao ndi aneneri ao, onsewo adzachita manyazi. Amauza mtengo kuti ‘Iwe ndiwe bambo wathu,’ amauza mwala kuti ‘Iwe ndiwe amene udatibala.’ Koma Ine amandifulatira, m'malo motembenukira kwa Ine. Tsono akakhala pa mavuto amati, ‘Dzambatukani, mutithandize.’ Nanga milungu yanu ili kuti, milungu ija mudadzipangira ija? Idzambatuketu, ngati ingathe kukupulumutsani pa nthaŵi yanu ya mavuto. Inu anthu a ku Yuda, milungu yanu ndi yambiri, kuchuluka kwake monga momwe iliri mizinda yanu.” Chauta akuti, “Kodi mukundiimbiranji mlandu? Nonsenu mwandipandukira. Ndidalanga ana anu popanda phindu, sadaphunzirepo nkanthu komwe. Monga mkango wolusa mudapha aneneri anu ndi lupanga.” Inu anthu amakono, imvani mau a Chauta. “Kodi ndakhala ngati chipululu kwa Israele, kapena ngati dziko la mdima wandiweyani? Chifukwa chiyani tsono anthu anga akunena kuti, ‘Ndife mfulu, sitidzabweranso kwa Inu?’ Kodi namwali amaiŵala zokongoletsera zake, kapena mkwati kuiŵala zovala zake zaukwati? Komabe anthu anga andiiŵala Ine masiku osaŵerengeka. “Mumadziŵa bwino njira zopezera zibwenzi zam'seri. Ngakhale akazi oipa kwambiri omwe mumaŵaphunzitsa ndinu. Zovala zanu zili psu ndi magazi a anthu osauka osachimwa. Anthuwo simudaŵapeze nathyola nyumba. Komabe, ngakhale zinthu zili choncho, inu mukunena kuti, ‘Ndife osalakwa, mkwiyo wa Chauta wapola tsopano!’ Ine ndidzakuimbanibe mlandu chifukwa chonena kuti simudachimwe. Bwanji mukudzipeputsa nokha posinthasintha njira zanu! Ejipito adzakugwiritsani mwala monga muja adakuchititsirani manyazi Aasiriya. Mudzatuluka kumeneko aliyense atagwirira manja ku mutu. Ine Chauta ndidaŵakana amene inu mumagonerapo, ndipo anthuwo sadzakuthandizani mpang'ono pomwe.” Chauta akuti, “Munthu akasudzula mkazi wake, mkaziyo nkuchoka, nakakwatiwa ndi mwamuna wina, kodi mwamuna woyambayo angathe kumtenganso mkaziyo? Kodi atachita zotero, sindiye kuti dzikolo laipitsidwa kwambiri? Tsono iwe Israele, wachita zadama ndi abwenzi ambiri. Kodi ungabwererenso kwa Ine? Uyang'ane ku zitunda zonse zachipembedzo. Mpoti pamene sudachitepo zadama? Unkakhala m'mbali mwa njira kumadikirira zibwenzi zako, ngati Mluya wobisalira anthu m'chipululu. Waipitsa dziko ndi mkhalidwe wako woipa wachiwerewere. Nchifukwa chake Chauta adaimitsa mvula, ndi mvula yam'masika yomwe sidagwe. Komabe maonekedwe ako onse nga mkazi wachiwerewere, ndipo ulibe ndi manyazi omwe. Kodi si tsopano apa wakhala ukundiwuza kuti, ‘Atate, ndinu bwenzi la unyamata wanga,’ numadzifunsa kuti, ‘Kodi Chauta adzandipsera mtima nthaŵi zonse? Kodi adzakwiya mpaka muyaya?’ Umu ndimo m'mene unkalankhulira. Komabe iwe udapitiriza kuchita zoipa monga momwe unkathera.” Pa nthaŵi ya mfumu Yosiya, Chauta adati, “Kodi waona zimene wosakhulupirika uja Israele adachita? Ankakwera kukapembedza pa phiri, ndi patsinde pa mtengo uliwonse wogudira. Motero kumeneko ankakachita zadama. Ndidaaganiza kuti atachita zonsezi, adzabwerera kwa Ine, koma sadabwerere. Tsono Yuda, mbale wake wosakhulupirika uja, adaziwona zimenezo. Adaona kuti Israele wosakhulupirika uja ndidamsudzula ndi kumpirikitsa chifukwa cha zigololo zake. Komabe Yuda, mbale wake, sadaope. Iyenso adakhala wosakhulupirika, adapita kukachita zadama. Dama la Israele linali lochititsa manyazi, kotero kuti potsiriza pake adaipitsa dziko. Adachita chigololo popembedza mafano amiyala ndi amitengo. Komabe atachita zonsezi, Yuda mbale wake wosakhulupirika uja sadabwerere kwa Ine ndi mtima wonse, koma mwachiphamaso chabe,” akuterotu Chauta. Chauta adandiwuzanso kuti, “Israele wosakhulupirika uja kupalamula kwake nkochepa, kuyerekeza ndi Yuda wosakhulupirika uja. Pita ukalalike kumpoto uthenga uwu wakuti, “ ‘Israele wosakhulupirikawe, bwerera,’ akuterotu Chauta. ‘Ukali wanga sudzapitirira, poti ndine wachifundo. Sindidzakukwiyira mpaka muyaya. Ungovomera kulakwa kwako. Vomera kuti udaukira Chauta Mulungu wako, kuti udapembedza nao milungu yachilendo patsinde pa mitengo yogudira, ndiponso kuti sudamvere mau anga,’ ” akuterotu Chauta. “Bwererani inu anthu osakhulupirika, pakuti mbuye wanu ndine. Ndidzakutengani kupita nanu ku Ziyoni, mmodzi kuchokera ku mzinda uliwonse, aŵiri kuchokera ku banja lililonse. “Kumeneko ndidzakupatsani abusa a kukhosi kwanga. Adzakutsogolerani mwanzeru ndi mwaluntha. Masiku amenewo mukadzachulukana m'dzikomo, anthu sadzalankhulanso za bokosi lachipangano la Chauta. Sadzaliganizira kapena kulikumbukira kapena kulisoŵa, ndipo sadzapanganso lina. Nthaŵi imeneyo Yerusalemu adzatchulidwa Mpando waufumu wa Chauta. Ndipo mitundu yonse ya anthu idzasonkhana kumeneko pamaso pa Chauta. Sadzaumiriranso kutsata mtima wao woipa. Masiku amenewo fuko la Yuda lidzaphathana ndi fuko la Israele. Onse pamodzi adzachokera ku dziko lakumpoto kupita ku dziko limene ndidapatsa makolo ao, kuti likhale choloŵa.” Chauta akunena kuti, “Iwe Israele, ndikadakonda kukukhazika pakati pa ana anga, ndi kukupatsa dziko lokoma, choloŵa chokongola kwambiri kupambana maiko a mitundu ina ya anthu. Ndidaganiza kuti udzanditchula ‘Atate’, ndipo kuti sudzaleka kumanditsata. Ndithu, monga momwe mkazi wosakhulupirika amasiyira mwamuna wake, iwenso Israele wakhala wosakhulupirika kwa Ine,” akuterotu Chauta. Pakumveka liwu pa magomo, Aisraele akulira ndiponso akupempha chifundo, pakuti atsata njira zoipa, ndipo aiŵala Chauta, Mulungu wao. “Bwererani kwa Ine, inu anthu anga osakhulupirika. Ndidzakuchiritsani kuti mukhale okhulupirika.” Inu mukuti, “Tikubwera kwa Inu, poti ndinu Chauta, Mulungu wathu. Kupembedza pa magomo sikuthandiza, kuchita maphwando pa mapiri kulibenso ntchito. Zoonadi, mwa Chauta, Mulungu wathu ndiye muli chipulumutso cha Israele. “Kuchokera pa chiyambi cha mtundu wathu, Baala, mulungu wochititsa manyazi uja, wakhala akutiwonongetsa phindu la ntchito ya makolo athu, ndiye kuti nkhosa ndi ng'ombe zao, ana ao aamuna ndi ana ao aakazi. Tsono tigone pansi mwamanyazi, ndipo kunyozeka kwathu kutiphimbe. Paja tidachimwa ife pamodzi ndi makolo athu, kuchimwira Chauta Mulungu wathu, kuyambira ubwana wathu mpaka lero lino. Sitidamvere mau a Chauta Mulungu wathu.” “Ngati mukufuna kubwerera, inu Aisraele, bwererani kwa Ine,” akuterotu Chauta. “Chotsani mafano anu amene akundinyansaŵa, ndipo musasokerenso. Muzilumbira moona kuti, ‘Pali Chauta wamoyo.’ Muzichita zimenezi mwachilungamo ndi mokhulupirika. Mukatero, anthu a mitundu yonse adzandipempha kuti ndiŵadalitse, ndipo adzanditamanda.” Chauta akuuza anthu a ku Yuda ndi anthu okhala ku Yerusalemu kuti, “Limani masala anu, musabzale pakati pa minga. Muzikhala okhulupirika ndi kumanditumikira Ine Chauta ndi mtima wanu wonse. Muzichita zimenezi inu anthu a ku Yuda ndi inu okhala ku Yerusalemu, kuwopa kuti mkwiyo wanga ungabuke ngati moto, ndi kukuyakirani chifukwa cha ntchito zanu zoipa, osapezeka wina aliyense wotha kuuzimitsa.” Lalika ku Yuda, lengeza ku Yerusalemu kuti, “Lizani lipenga m'dziko lonse, ndi kufuula kuti, ‘Sonkhanani, tiyeni tipite ku mizinda ku Ziyoni.’ Kwezani mbendera ku Ziyoni. Musachedwe, thaŵani kuti mupulumuke. Chauta akubweretsa chilango kuchokera kumpoto, kudzakhala chiwonongeko chachikulu. Monga momwe mkango umatulukira m'ngaka yake, momwemonso woononga maiko wanyamuka. Watuluka m'malo mwake kuti asakaze dziko lanu. Mizinda yanu idzakhala mabwinja popanda okhalamo. Motero valani ziguduli, mudandaule ndi kulira kwambiri. Pakuti mkwiyo woopsa wa Chauta sudatichoke.” Chauta akuti, “Pa tsiku limenelo mfumu ndi nduna zake, onse adzataya mtima. Ansembe adzaopsedwa, ndipo aneneri adzangoti kakasi.” Tsono ndidati, “Ha, Ambuye Chauta, ndithu mudaŵanyenga anthu aŵa pamodzi ndi a mu Yerusalemu! Mudaŵauza kuti, ‘Mudzakhala pa mtendere,’ koma chonsecho lupanga lili pamutu pao.” Nthaŵiyo ikadzafika, anthu a mu Yerusalemu adzaŵauza kuti, “Mphepo yotentha yochokera ku magomo am'chipululu ikukuntha pa anthu anga, osatitu mphepo yopetera kapena kuyeretsera zinthu ai. Imeneyo ndi mphepo yamphamvu zedi yochokera kwa Ine Mulungu. Ndipo ndi Ineyo amene ndikuŵaimba mlandu.” Onani, adani akubwera mwaliŵiro ngati mitambo, magaleta ao akuthamanga ngati kamvulumvulu. Akavalo ao ngaliŵiro kuposa chiwombankhanga. Kalanga ine, taonongeka. Iwe Yerusalemu, chotsa zoipa mumtima mwako kuti upulumuke. Kodi maganizo ako oipa udzakhala nawobe mpaka liti? Pakuti amithenga a ku Dani akulalika mau, akulengeza zoopsa kuchokera ku Phiri la Efuremu. Akuti, “Muchenjeze mitundu ya anthu kuti mdani akubwera. Mulengeze kwa anthu a mu Yerusalemu kuti ankhondo akubwera kuchokera ku dziko lakutali, akufuula ndi kudzathira nkhondo mizinda ya Yuda. Akuzinga Yerusalemu ngati alonda a munda, chifukwa choti anthu andipandukira,” akuterotu Chauta. “Zimenezi zakugwerani, inu Ayuda, chifukwa cha makhalidwe anu oipa ndi zochita zanu. Chimenechi ndiye chilango chanu, nchoŵaŵa kwambiri, chokalasa mpaka ku mtima.” Mayo, mayo, ati kupweteka ati! Ha, mtima wanga ukuŵaŵa, ukugunda moti thithithi. Sindingathe kukhala chete. Ndikumva kulira kwa lipenga ndi mfuu yankhondo. Tsoka limatsata tsoka linzake, ndipo dziko lonse lasanduka bwinja. Mwadzidzidzi mahema athu aonongeka, machinga ake agwetsedwa pa kanthaŵi kang'onong'ono. Kodi ndikhale ndikuwona mbendera yankhondo mpaka liti? Kodi ndikhale ndikumva lipenga mpaka liti? Chauta akuti “Paja anthu anga ndi opusa, Ine sandidziŵa. Ali ngati ana opulukira, osamvetsa chilichonse. Ali ndi luso pochita zoipa, koma kuchita zabwino sadziŵa.” Ndidayang'ana dziko lapansi, linali lopanda anthu ndi lopanda kanthu kalikonse. Ndidayang'ana thambo, linalibe konse kuŵala. Ndidayang'ana mapiri, ankagwedezeka, ndipo magomo onse ankangosunthira uku ndi uku. Ndidayang'ana, osaona ndi munthu mmodzi yemwe, ndipo mbalame zonse zamumlengalenga zinali zitathaŵa. Ndidayang'ana, dziko la chonde linali litasanduka chipululu, mizinda yake yonse inali itasanduka mabwinja, chifukwa cha mkwiyo wa Chauta. Chauta akunena kuti, “Dziko lonse lidzasanduka chipululu, komabe sindidzaliwononga kotheratu. Chifukwa cha zimenezi dziko lonse lapansi lidzalira ndipo zakumwamba zidzachita mdima. Pakuti Ine ndalankhula, ndipo ndili ndi cholinga. Sindidafeŵe mtima, ndipo sindidzabwerera konse m'mbuyo.” Anthu a m'mudzi uliwonse adzathaŵa, pakumva phokoso la ankhondo okwera pa akavalo ndi oponya mivi. Azikati uku ena akuloŵa m'nkhalango, ena akukwera m'mathanthwe. Mizinda yonse kuisiya, popanda ndi mmodzi yemwe wokhalamo. Iwe Yerusalemu, ndiwe bwinja. Ukuti utani m'mene ukuvala zofiira, m'mene ukuvala zokongoletsa zagolide, m'mene ukukuza maso ako poŵapaka zokometsera? Ukungodzivuta poyesa kudzikongoletsa. Zibwenzi zako zikukunyoza, zikufuna kulanda moyo wako. Ndidamva kulira ngati kwa mkazi pa nthaŵi yake yochira, kubuula ngati kwa mkazi pa uchembere wake woyamba. Kumeneku kunali kulira kwa anthu a mu Ziyoni, ŵefuŵefu, atatambalitsa manja ao, akunena kuti, “Tsoka ife! Tikukomoka, moyo wathu waperekedwa kwa anthu otipha.” “Thamangani uku ndi uku m'miseu ya Yerusalemu, mudziwonere nokha. Funafunani ku mabwalo ake ngati mungapezeke munthu, munthu wake wochita zolungama, wofunitsitsa zoona, kuti choncho Yerusalemu ndidzamkhululukire. Ngakhale anthu akulumbira m'dzina la Chauta wamoyo, komabe akungolumbira monama. Kodi Inu Chauta, suja mumafuna anthu onena zoona? Inu mudaŵakantha anthuwo, koma iwo sadamve kuŵaŵa. Mudaŵatswanya, koma sadafune kutembenuka mtima. Adaumitsa mitima yao ngati mwala, adakana kwamtuwagalu kulapa.” Apo ndidati, “Ndi amphaŵi chabe aŵa, alibe ndi nzeru zomwe. Iwo sadziŵa njira ya Chauta, sazindikira zimene Mulungu wao akufuna. Tsono ndidzapita kwa akuluakulu, ndidzalankhula ndi amenewo. Pakuti ndiwo angadziŵe njira ya Chauta, ndi zimene Mulungu wao akufuna.” Koma ndidaona kuti iwowonso adathyola goli la Chauta, adadula nsinga zao. Nchifukwa chake mkango wam'malunje udzaŵapha, mmbulu wochoka ku thengo udzaŵaononga. Kambuku adzaŵalalira pafupi ndi mizinda yao. Ndipo adzakadzula aliyense wotuluka, poti zolakwa zao nzambiri, abwereratu m'mbuyo kwambiri. Chauta akuti, “Kodi ndingakukhululukireni bwanji pa zonsezi? Ana anu adandisiya Ine, ndipo adapembedza milungu imene siili milungu konse. Ine ndidaŵapatsa zonse zimene ankasoŵa, komabe adakonda kumachita chigololo, namapita ku nyumba za akazi adama. Aliyense ankathamangira mkazi wa mnzake, monga amachitira akavalo onenepa akamamemesa. Ndiye ndingapande kuŵalanga chifukwa cha zimenezi? Monga ndisaulipsire mtundu wochita zotere? Tsono ndidzatuma adani kuti akaononge mizere ya mipesa yao, komabe osati kotheratu. Akasadze nthambi zake, poti anthu ameneŵa si ake a Chauta. Anthu a ku Israele ndi a ku Yuda onse akhala osakhulupirika kwa Ine,” akuterotu Chauta. Anthuwo ankanama ponena za Chauta, ankati, “Mulungu sangatichite kanthu. Choipa sichidzatigwera, sitidzaona nkhondo kapena njala. Mau a aneneri azikangopita ngati mphepo, ndipo uthenga wao si wa kwa Mulungu. Zimene amanena zidzaŵagwera iwo omwewo.” Nchifukwa chake tsono Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, akuti, “Poti iwowo atero, mau anga ndidzaŵasandutsa moto m'kamwa mwako, anthuwo ndidzaŵasandutsa nkhuni, ndipo motowo udzaŵapserezeratu.” “Iwe Israele, ndikukudzetsera mtundu wa anthu odzakuthira nkhondo, mtundu wake ndi wochokera kutali. Mtundu umenewu ndi wosagonjerapo, mtundu wakalekale, mtundu umene chilankhulo chake iwe suchidziŵa, ndipo zimene akunena, iwe sungazimvetse. Ankhondowo mipaliro yao imapha anthu ambirimbiri, onsewo ndi ngwazi zokhazokha pa nkhondo. Adzakutherani zokolola zanu ndi chakudya chanu. Adzapha ana anu aamuna ndi aakazi, adzakupheraninso nkhosa zanu ndi ng'ombe zanu. Adzaononga mipesa yanu ndi mikuyu yanu. Adzagwetsa mwankhondo mizinda yanu yamalinga imene mumaidalira. “Koma ngakhale pa masiku amenewo sindidzakuwonongani kotheratu. Ndipo mukamafunsana kuti, ‘Chifukwa chiyani Chauta Mulungu wathu watichita zimenezi?’ Iwe Yeremiya uzidzayankha kuti, ‘Monga momwe mudasiyira Chauta, ndi kumatumikira milungu yachilendo m'dziko lanu, momwemonso ndimo m'mene inuyo muzidzatumikira anthu a m'dziko lachilendo.’ ” Mulalike kwa ana a Yakobe, mulengeze kwa anthu a ku Yuda kuti, “Imvani izi, inu anthu opusa, opanda ndi nzeru zomwe, inu amene maso muli nawo, koma simupenya, amene makutu muli nawo, koma simumva. Ine Chauta ndikuti, Kodi simukuchita nane mantha? Kodi simukunjenjemera pamaso panga? Ndine amene ndidaika mchenga kuti ukhale malire a nyanja, malire amene nyanjayo singaŵabzole. Mafunde ake, ngakhale aŵinduke bwanji, sangathe kupitirirapo. Ngakhale akokome chotani, sangathe kubzola. Koma anthu ameneŵa ndi okanika ndiponso a mtima waupandu. Adapatuka ndipo adapitiratu. Sadanenepo m'mitima mwao kuti, ‘Tiyeni tizimvera Chauta Mulungu wathu, amene amatipatsa mvula pa nthaŵi yake, mvula yachizimalupsa ndi yam'masika. Ndipo salephera kutipatsa nthaŵi ya kholola.’ ” Koma zolakwa zanu zaletsetsa zonsezi, ndipo machimo anu akumanitsani zokoma. Paja mwa anthu anga muli ena achifwamba, amene amalalira anzao monga m'mene amachitira otchera mbalame. Amatcha misampha nakola anthu. Nyumba zao nzodzaza ndi chuma chochipeza mwachinyengo, ngati chitatanga chodzaza ndi mbalame. Nchifukwa chake adasanduka otchuka ndi olemera. Adanenepa nkukhala a matupi osalala. Ntchito zao zoipa nzopanda malire, saweruza mwachilungamo nkhani ya ana amasiye, kuti iyende bwino, ndipo sateteza amphaŵi. Chauta akuti, “Ndiye ndingapande kuŵalanga chifukwa cha zimenezi? Monga ndisaulipsire mtundu wochita zotere?” M'dziko muno mwachitika chinthu chododometsa ndi choopsa. Aneneri akulosa zabodza, ndipo ansembe akuvomerezana nawo. Komabe anthu anga akukondanso zomwezo. Kodi mudzatani potsiriza? Inu anthu a ku Benjamini thaŵani, tulukanimo m'Yerusalemu. Lizani lipenga ku Tekowa, kwezani mbendera ku Betehakeremu. Tsoka likudzakugwerani kuchokera kumpoto, ndipotu nchiwonongeko chachikulu. Ndidzauwononga mzinda wa Ziyoni, mzinda wooneka bwino ndi wokongola. Mafumu adzabwera ndi asilikali ao. Adzamanga zithando momzinga Yerusalemu, ndipo aliyense adzakhazika anthu ake pamalo pake. Adzanena kuti, “Konzekani kuti muuthire nkhondo mzindawu. Bwerani tiwuthire nkhondo masana ano.” “Koma tili ndi tsoka, dzuŵa lapendeka, zithunzithunzi zakumadzulo zikunka zitalika.” “Bwerani tsono tiwuthire nkhondo usiku uno, tiwononge malinga ake.” Mau a Chauta Wamphamvuzonse akuti, “Gwetsani mitengo ya mu Yerusalemu, ndipo mzindawu muumangire nthumbira zankhondo. Mzinda umenewu ndi woyenera kulangidwa, anthu ake amangokhalira kuzunzana. Monga momwe chitsime chimasungira madzi ake, ndimonso m'mene mzindawo umasungira zoipa zake. Zimene mukumva ndi za chiwonongeko ndi za nkhondo. Ndikuwonamonso matenda ndi zilonda. Iwe Yerusalemu, tengapo phunziro, kuwopa kuti chikondi changa pa iwe chingathe, ndipo ndingakusandutse dziko lachipululu, dziko lopanda anthu.” Mau a Chauta Wamphamvuzonse akuti, “Akunkheni ndi kuŵalanda zonse anthu otsala a Aisraele, monga momwe anthu amachitira, populula mphesa ku nthambi zake.” Kodi ndilankhule ndi yani, ndipo ndichenjeze yani, kuti amve? Makutu ao ndi otsekeka, sangathe kumva. Mau a Chauta amaŵanyoza kwambiri, saŵalabadira konse. Nchifukwa chake ndadzazidwa ndi mkwiyo wa Chauta, sindingathenso kudzimanga kuti usatulukire kunja. Chauta akuti, “Mkwiyo umenewu ukauthire pa ana oyenda mu mseu, ndi pa achinyamata kumene amasonkhanira. Mwamuna ndi mkazi wake adzatengedwa, ngakhale aimvi ndi okalamba kwambiri. Nyumba zao zidzapatsidwa kwa ena pamodzi ndi minda yao ndi akazi ao omwe. Ndithuditu, ndi dzanja langali ndidzakantha anthu okhala m'dzikomo. “Pakuti onse, ang'onoang'ono ndi akuluakulu omwe, ali ndi khwinthi la phindu lopeza mwakuba. Aneneri pamodzi ndi ansembe ao, onsewo ndi onyenga. Iwo amapoletsa mabala a anthu anga pamwamba pokha. Amangonena kuti, ‘Kuli mtendere, kuli mtendere,’ chonsecho kulibe konse mtendere. Kodi akamachita zonyansa, amachita manyazi ngati? Iyai, sachita manyazi mpang'ono pomwe. Sadziŵa nkugwetsa nkhope komwe. Nchifukwa chake adzagwera pakati pa anzao amene adagwa kale. Adzagweratu pa tsiku limene ndidzaŵalanga!” Akutero Chauta. Mau a Chauta ndi aŵa, “Imani pa mphambano, ndipo mupenye. Mufunse kumene kuli njira zakale ndi kumene kuli njira yabwino. Tsono mutsate njira yabwinoyo, ndipo mudzakhala pa mtendere. Koma inuyo mudati, ‘Sitidzaitsata.’ Chauta adakupatsani alonda oti akutsogolereni nati, ‘Imvani kulira kwa lipenga lokuchenjezani.’ Koma inu mudati, ‘Sitidzasamalako.’ Nchifukwa chake imvani inu anthu a mitundu ina, penyetsetsani, inu mwasonkhana panonu, zimene zidzaŵagwere anthuwo. Tamvani inu okhala pa dziko lapansi, anthuwo ndidzaŵaononga. Komatu zimenezo nzotsatira za kunyenga kwao, chifukwa sadamvere mau anga ndipo sadamvere malamulo anga. Kodi pali phindu lanji kwa Ine, ngakhale abwere ndi lubani kuchokera ku Sheba, kapena zonunkhira zina kuchokera ku maiko akutali? Sindidzalandira zopereka zao zopsereza, nsembe zao sizindikondwetsa. Nchifukwa chake anthu ameneŵa ndidzaŵaikira zoŵakhumudwitsa. Atate ndi ana ao aamuna, anansi ndi abwenzi ao, onsewo adzaonongeka.” Chauta akunena kuti, “Onani, anthu a mtundu wina akubwera kuchokera ku dziko lakumpoto. Mtundu wa anthu amphamvu wanyamuka kuchokera mbali zakutalitali za dziko lapansi. Atenga mauta ndi mikondo, ndi anthutu ankhalwe ndi opanda chifundo. Phokoso lao lili ngati mkokomo wa nyanja. Akwera pa akavalo, akonzekera ngati munthu wankhondo, akudzamenyana nawe, iwe Ziyoni.” A ku Yerusalemu akuti, “Mbiri ya iwowo taimva, m'nkhongono mwati zii. Nkhaŵa yatigwira, ndipo tikumva ululu wonga wa mkazi panthaŵi yake yochira.” Musayesere kupita ku minda, kapena kuyenda pa mseu, pakuti adani akubwera ndi nkhondo ndipo ponseponse pali mantha okhaokha. Inu anthu anga, valani ziguduli, gubuduzikani pa phulusa. Lirani kwamphamvu, ngati munthu wolira mwana wake mmodzi yekha, pakuti mwadzidzidzi woononga adzabwera kudzakuphani. “Iwe Yeremiya, ndakusankha kuti ukhale choyesera zitsulo. Uŵayese anthu anga kuti uwone m'mene aliri makhalidwe ao. Onsewo ali ndi upandu wokanika, onsewo ndi akazitape, ndi olimba ngati mkuŵa ndi chitsulo. Onse amangochita zoipa zokhazokha. Mvukuto zikuuzira kwambiri, mtovu wasungunuka ndi moto. Koma ntchito yosungunulayo sikupindula, chifukwa choti dothi loipa silikuchokapo. Iwo ali ngati siliva wotaya, pakuti Chauta waŵakana.” Chauta adauza Yeremiya mau aŵa akuti, “Ima pa chipata cha Nyumba ya Chauta ndipo kumeneko ukalalike kuti: Imvani mau a Chauta, inu nonse anthu a ku Yuda, amene mumaloŵa pa chipata ichi kudzapembedza Chauta. Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akukuuzani kuti, Konzani makhalidwe ndi zochita zanu, ndipo ndidzakulolani kumakhala pa malo ano. Musamangodzinyenga ndi maganizo akuti muli pabwino ponena kuti, ‘Malo ano ndi Nyumba ya Chauta, Nyumba ya Chauta, Nyumba ya Chauta!’ “Konzani makhalidwe anu ndi zochita zanu. Muzichitirana zolungama. Musazunze alendo kapena ana amasiye kapena akazi amasiye. Musaphe anthu osachimwa pa malo ano. Musamatsate milungu ina, kuti ingakuwonongeni. Mukamvera mau anga, ndidzakulolani kuti mukhale pa malo ano, m'dziko limene ndidapatsa makolo anu mpaka muyaya. “Koma onani, inu mumakhulupirira mabodza. Mumaba, mumapha, mumachita zigololo, mumalumbira zonama, mumapereka nsembe zopsereza kwa Baala, mumatsata milungu ina imene kale simunkaidziŵa. Pambuyo pake mumabwera kudzaima pamaso panga m'Nyumba ino, Nyumba imene imadziŵika ndi dzina langa. Mumanena kuti, ‘Tapulumuka ife,’ koma mumapitirirabe kumangochita zonyansa zonsezi. Kodi tsopano Nyumba ino, Nyumba imene imadziŵika ndi dzina langayi, yasanduka phanga lobisalamo mbala zachifwamba, inu mukuwonerera? Mwiniwakene ndaziwona zonsezi,” akuterotu Chauta. “Pitani ku malo anga ku Silo, malo amene poyamba ankadziŵika ndi dzina langa. Mukaone zimene ndidachita kumeneko chifukwa cha kuipa kwa anthu anga Aisraele. Munkachita zoipa zonsezi, mudakana kundimvera nditakulankhulani kosalekeza, ndipo simudayankhe pamene ndidakuitanani. Nchifukwa chake zomwe ndidachita ku Silo, ndidzachitanso ku Nyumba ino, imene imadziŵika ndi dzina langa, malo amene inu mumaŵakhulupirira, malo amene ndidakupatsani inu pamodzi ndi makolo anu. Ndidzakuchotsani pamaso panga monga momwe ndidachotsera abale anu onse, zidzukulu zonse za Efuremu. “Iwe Yeremiya, usaŵapempherere anthu ameneŵa. Usaŵapepesere kwa Ine kapena kuŵadandaulira mondiwumiriza chifukwa Ine sindikumvera. Kodi sukuwona zimene zikuchitika m'mizinda ya ku Yuda ndi m'miseu ya m'Yerusalemu? Ana akutolera nkhuni, atate akusonkha moto, akazi akukanda ufa kuti aphike makeke, kuchitira ulemu amene amati ndi mfumukazi yakumwamba. Iwowo amathira nsembe yazakumwa kwa milungu ina, kuti andipsetse mtima. Amati atani! Amayesa kuti akuvuta Ine, koma akungodzivuta okha ndi kumadzichititsa manyazi. Nchifukwa chake ndidzaŵalanga koopsa mwaukali. Mkwiyo wanga udzagwera Nyumba yangayi, anthu, nyama, mitengo ndi mbeu zomwe. Mkwiyowo udzayaka ngati moto wosazimika.” Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, “Muwonjeze zopereka zanu zopsereza pa nsembe zanu zinazo, ndipo mudye nyama yake. Pamene ndidatulutsa makolo anu ku dziko la Ejipito, sindidaŵalamule kuti azipereka nsembe zopsereza kapena nsembe zina. Koma chimene ndidaalamula nchimodzi, ndidati, ‘Mukamandimvera, ndidzakhala Mulungu wanu, ndipo inu mudzakhala anthu anga. Muzitsata malamulo anga onse kuti zinthu zikukomereni!’ Koma anthuwo sadamvere, sadasamaleko, ndipo adapitirira kukhala osamvera ndi mitima yao yoipa. Adayang'ana zam'mbuyo osati zakutsogolo. Kuyambira tsiku limene makolo anu adatuluka ku dziko la Ejipito mpaka lero lino, ndakhala ndikukutumizirani atumiki anga aneneri kaŵirikaŵiri. Komabe inu simudandimvere, simudasamaleko. Ndi mitima yanu yokanika, mwaipa kupambana makolo anu. “Iwe ungaŵauze zimenezi, sadzakumvera. Ungaŵaitane, sadzakuyankha. Nchifukwa chake udzaŵauze kuti, ‘Uwu ndi mtundu wa anthu uja sadamvere mau a Chauta Mulungu wao, ndipo sadafune kukonzeka. Mau oona atheratu ndipo pakamwa pamangonena zonama zokhazokha.’ “Meta tsitsi lako, ndipo ulitaye. Ulire kwambiri pa zitunda zopanda zomera, poti Chauta waukana mbadwo uwu umene wamkwiyitsa. Anthu amenewo Iye waŵasiyadi.” Chauta akuti, “Anthu a ku Yuda achita zoipa Ine ndikuwona. Aimika mafano ao onyansa m'Nyumba ino imene imadziŵika ndi dzina langa, ndipo aiipitsa. Amanga nsanja yotchedwa Tofeti m'chigwa cha Benihinomu, kuti atenthereko ana ao aamuna ndi aakazi. Zimenezo sindidalamule konse, ngakhale kuziganiza komwe. Nchifukwa chake nthaŵi ikubwera pamene malo ano sadzatchedwanso Tofeti, kapena za Chigwa cha Benihinomu, koma za Chigwa cha Chipheiphe, pakuti anthu akufa adzaŵaika ku Tofeti, chifukwa choti sikudzapezekanso malo owaika. Tsono mitembo ya anthu ameneŵa idzakhala chakudya cha mbalame zamumlengalenga ndi zilombo zakuthengo. Ndipo palibe wina amene adzazipirikitse. Sikudzamvekanso mau achisangalalo ndi achimwemwe ku mizinda ya ku Yuda ndi ku miseu ya mu Yerusalemu. Sikudzamvekanso mau achikondwerero, a mkwati wamwamuna ndi wamkazi. Ndithudi dzikolo lidzasanduka chipululu.” Chauta akunena kuti, “Pa nthaŵi imeneyo anthu adzatulutsa m'manda mafupa a akalonga, a ansembe, a aneneri ndiponso a anthu onse amene ankakhala ku Yerusalemu. Adzaŵamwaza pa mtunda kuyang'ana mwezi, ndi nyenyezi zonse zakumwamba zimene ankazikonda, kumazitumikira, kuzitsata, kuzipempha nzeru ndi kumazipembedza. Mafupa amenewo sadzaŵasonkhanitsa kapena kuŵakwirira, koma adzasanduka ndoŵe pamwamba pa nthaka. Anthu onse otsala mwa anthu a mtundu woipawu, kulikonse kumene ndaŵapirikitsira, adzakonda kufa kupambana kuti akhale ndi moyo,” akuterotu Chauta Wamphamvuzonse. Chauta adandiwuza kuti ndifunse anthu ake mau aŵa: “Kodi anthu akagwa, ndiye kuti sangathe kudzukanso? Kodi munthu akasokera, ndiye kuti sangathe kubwereranso? Chifukwa chiyani nanga anthu ameneŵa akupitirirabe kulakwa, osabwereranso? Akangamira ndithu machimo ao, akukana kubwerera. Ndakhala ndikutchereza ndi kuŵamvetsera, koma sadalankhulepo zoona. Palibe wochimwa aliyense amene adandiwonetsa kuti walapa, namanena kuti, ‘Ndachitanji ine?’ Koma aliyense akungotsata njira zake, ngati kavalo wothamangira nkhondo. Mbalame amati kapande ija imadziŵa nthaŵi yake mumlengalenga. Nkhunda, namzeze ndi ngalu zimadziŵa nthaŵi yake yonyamukira ulendo. Koma anthu anga sadziŵa malangizo a Chauta. “Mungathe kunena bwanji kuti, ‘Ndife anzeru, timasunga malamulo a Chauta, pamene alembi akulemba zabodza?’ Anthu anzeru adzachita manyazi, adzatha nzeru, ndipo adzagwidwa. Akana mau a Chauta, nanga nzeru zao nzotani? Nchifukwa chake akazi ao ndidzaŵapatsa kwa anthu ena, minda yao ndidzaipereka kwa amene aŵagonjetsa. Ndithudi, kuyambira ana ndi akulu omwe, onsewo ali ndi khwinthi la phindu lopeza monyenga. Aneneri ndi ansembe omwe, onsewo ndi onyenga. Iwo amapoletsa mabala a anthu anga pamwamba pokha. Amangonena kuti, ‘Kuli mtendere, kuli mtendere,’ chonsecho kulibe konse mtendere. Kodi akamachita zonyansa, amachita manyazi ngati? Iyai, sankachita manyazi mpang'ono pomwe. Sadziŵa nkugwetsa nkhope komwe. Nchifukwa chake adzagwera pakati pa anzao amene adagwa kale. Adzagweratu pa tsiku limene ndidzaŵalanga,” akutero Chauta. “Ndidzaŵatheratu. Ndidzachotsa dzinthu dza m'minda mwao. Sipadzakhala mphesa pa mpesa, kapena nkhuyu pa mkuyu, ndi masamba ake omwe adzauma. Zinthu zimene ndidaŵapatsa, ndidzaŵachotsera zonse.” Anthu amati, “Chifukwa chiyani tikungokhala? Tiyeni tonse pamodzi tithaŵire ku mizinda yamalinga, tikafere komweko. Chauta, Mulungu wathu, wagamula kuti tiyenera kufa, watimwetsa madzi aululu pakuti tamchimwira. Tinkafuna mtendere, koma zinthu sizidatiyendere bwino. Tinkafuna kuchira, koma tidangopeza zoopsa zokhazokha.” “Adani athu aloŵa kale mu mzinda wa Dani. Dziko lonse likunjenjemera ndi kulira kwa akavalo ao. Adani akubwera kudzaononga dzikoli pamodzi ndi zinthu zake zonse. Adzaononganso mzinda ndi onse okhalamo. Onani, ndikukutumirani njoka, mphiri zimene munthu sangazilodze, ndipo zidzakulumani,” akuterotu Chauta. Kudandaula kwanga nkosalekeza. Mtima wanga walefukiratu. Imvani kulira kwa anthu anga kuchokera ku dziko lakutali. Akuti, “Kodi Chauta sali ku Ziyoni? Kodi mfumu yake siili kumeneko?” Chauta ayankha kuti, “Chifukwa chiyani akundiputa ndi mafano ao, ndiponso ndi milungu yao yachilendo?” Anthu akuti, “Kholola lapita, chilimwe chapita, koma sitidapulumukebe.” Ndikumva kuŵaŵa chifukwa cha mavuto a anthu anga, ndikungolira, nkhaŵa yandigwira. Kodi ku Giliyadi kulibe mankhwala ochiritsa? Kodi kumeneko kulibe sing'anga? Chifukwa chiyani mabala a anthu anga sadapole? Ndikadakonda kuti mutu wanga ukhale ngati chitsime cha madzi, kuti maso anga akhale ngati kasupe wa misozi, kuti ndilire usana ndi usiku, kulirira onse amene adafa a mtundu wa anthu anga? Ndani adzandipatse pogona m'chipululu, kuti ndiŵasiye anthu anga ndi kuŵathaŵa. Paja onsewo ngachigololo, ndiponso ndi gulu la anthu onyenga. Amapinda lilime ngati uta. Dziko ladzaza ndi zabodza osati zoona. “Amanka naonjezeraonjezera zoipa, ndipo sandidziŵa Ine,” akuterotu Chauta. “Aliyense achenjere ndi mnzake, asakhulupirire ngakhale mbale wake. Zoona, aliyense amafuna kulanda malo a mbale wake. Aliyense amachitira mnzake ugogodi. Aliyense amanyenga mnzake, ndipo sanena zoona. Pakamwa pao adapazoloŵeza kulankhula zonama. Amakonda zoipa kwambiri, kotero kuti sangathenso kulapa. Amasanjikiza tchimo pa tchimo linzake, chinyengo pa chinyengo chinzake. Amakana kundidziŵa,” akuterotu Chauta. Nchifukwa chake Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Ndithu, anthu angaŵa ndidzaŵasungunula ngati chitsulo, ndipo ndidzaŵayesa. Iwowo ndi ochimwa, ndingathe bwanji kuŵalekerera? Lilime lao lili ngati muvi wakuthwa. Aliyense pakamwa pake pamatuluka mau aubwenzi, m'menemo mumtima mwake akukonzekera zomchita mnzake chiwembu. Kodi zimenezi ndipanda kuŵalanga nazo? Monga ndisaulipsire mtundu wotere wa anthu?” Akutero Chauta Ine ndidati, “Ndidzamva chisoni ndi kulira mokweza chifukwa cha mapiri. Ndidzadandaula chifukwa cha mabusa am'chipululu popeza kuti malo onsewo aonongeka. Palibe amene amapitako, sikumveka nkulira kwa ng'ombe komwe. Mbalame zonse zouluka ndiponso nyama zakuthengo zathaŵa, osaonekanso.” Apo Chauta adati, “Yerusalemu ndidzamsandutsa bwinja, ndidzamusandutsa mokhala nkhandwe. Mizinda ya ku Yuda idzasiyidwa, simudzakhala anthu.” Ine ndidati, “Kodi wanzeru ndani, amene angamvetse zimenezi? Chauta adazifotokozera yani, kuti iyeyo akafotokozere ena? Nanga chifukwa chiyani dziko laonongeka ndi kusanduka chipululu, m'mene anthu sapitamo?” Apo Chauta adayankha kuti, “Nchifukwa chakuti anthu angawo sadatsate malamulo amene ndidaŵapatsa, ndipo sadamvere mau anga ndi kuŵasamala. Koma ankangotsata zolakwa za mitima yao yokanika. Ankapembedza Abaala monga momwe makolo ao adaŵaphunzitsira. Tamvani tsono zimene Ine Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, ndidzachite. Anthu ameneŵa ndidzaŵadyetsa ziphe ndi kuŵamwetsa madzi azumu. Ndidzaŵabalalitsa pakati pa mitundu ya anthu imene iwowo kapena makolo ao sadaidziŵe. Ndidzaŵalondola ndi ankhondo mpaka kuŵatheratu onse.” Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Muziganize bwino, muitane akazi olira maliro kuti abwere. Akaziwo akhale aja amadziŵa kwambiri kuliraŵa.” Anthu akuti, “Abwere mofulumira adzatilire kuti m'maso mwathu mudze misozi nsidze zathu zinyowe.” Kukumveka kulira kwa Ziyoni, akuti, “Kalanga ife! Taonongeka! Manyazi aakulu atigwera. Tiyenera kusiya dziko lathu, chifukwa nyumba zathu azigwetsa.” Ine ndidati, “Inu azimai, mverani mau a Chauta. Tcherani makutu kuti mumve zimene akunena. Ana anu aakazi muŵaphunzitse kulira. Aliyense aphunzitse mnzake nyimbo yamaliro. Imfa yatifikira kudzera m'mawindo, yaloŵa ngakhale m'nyumba zathu zaufumu. Idapha ana athu m'miseu, ndipo idatha anyamata m'mabwalo.” Chauta adandiwuza kuti ndinene izi: “Mitembo ya anthu idzagwa, kuchita kuti mbwembwembwe ngati ndoŵe m'minda, ngati mitolo pambuyo pa anthu ovuna. Koma palibe amene adzaitole.” Chauta akunena kuti, “Munthu wanzeru asanyadire nzeru zake, munthu wamphamvu asanyadire mphamvu zake, ndipo munthu wolemera asanyadire chuma chake. Koma ngati wina afuna kunyadira, anyadire ichi chakuti amamvetsa za Ine, ndipo amandidziŵa. Amadziŵa kuti Ine ndine Chauta wokonda chifundo, chilungamo, ndi ungwiro pa dziko lapansi. Ndithudi, pazimenezi ndipo pali mtima wanga.” Chauta akunena kuti, “Nthaŵi ikubwera pamene ndidzalanga onse oumbalidwa, amene mu mtima sasamalako. Ndidzalanga Aejipito, Ayuda, Aedomu, Aamoni, Amowabu ndiponso onse amene amakhala m'chipululu namameta cham'mbali. Mitundu ina yonseyi njosaumbalidwa, ngakhale banja lonse la Israele nalonso nlosaumbalidwa mu mtima.” Inu Aisraele, imvani mau amene Chauta akukuuzani, Chauta akuti, “Musatsate makhalidwe a anthu a mitundu ina. Musachite mantha ndi zizindikiro zozizwitsa zamumlengalenga, ngakhale anthu a mitundu ina amachita nazo mantha zimenezi. Ndithudi, miyambo ya anthu a mitundu inayo nzopanda pake. Iwo aja amakadula mtengo ku nkhalango, munthu waluso namausema ndi nsompho. Anthu ena amakongoletsa chosemacho ndi siliva ndi golide, kenaka nkuchikhomerera ndi misomali, kuti chisagwedezeke. Mafano aowo ali ngati kangamunthu woopsera mbalame m'munda wa minkhaka, sangathe nkulankhula komwe. Ayenera kuŵanyamula, poti sangayende okha. Musaŵaope, chifukwa sangakuchiteni choipa. Alibenso mphamvu zochitira zabwino.” Palibe wolingana nanu, Inu Chauta. Inu ndinu aakulu, dzina lanu lili ndi mphamvu yaikulu. Ndani amene angaleke kukuwopani, Inu mfumu ya mitundu ya anthu? Paja kukuwopaniko nkokuyenerani. Pakati pa anthu anzeru onse ndiponso pakati pa maufumu onse a pansi pano palibe wina wolingana nanu. Onsewo ndi opusa ndi opanda nzeru. Nzeru zao amaphunzira ku mafano achabechabe opanga ndi mitengo. Siliva wosula wokutira mafanowo ndi wochokera ku Tarisisi, ndipo golide wake ndi wochokera ku Ufazi. Mafano aowo ndi ntchito ya anthu aluso ndi anthu odziŵa kuzokota golide. Amaveka mafanowo nsalu zonyezimira ndi zofiirira. Zonsezo ndi ntchito ya anthu aluso chabe. Koma Chauta ndiye Mulungu woona, Iyeyo ndiye Mulungu wamoyo ndiponso Mfumu yamuyaya. Dziko lapansi limagwedezeka ndi ukali wa Chauta. Anthu a mitundu ina sangathe kupirira ukali wakewo. Anthuwo mukaŵauze kuti, “Milungu imene sidalenge dziko lakumwamba ndi dziko lapansi, idzaonongeka ponseponse, pa dziko lapansi ndi pansi pa thambo.” Chauta ndiye amene adalenga dziko lapansi ndi mphamvu zake. Ndiye amene adapanga zonse ndi nzeru zake ndipo ndi umisiri wake adayala thambo lakumwamba. Iye akalankhula, kumamveka mkokomo wa madzi kumwamba, ndiye amene amadzetsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi. Amang'animitsa mphezi za mvula, amakunthitsa mphepo kuchokera kumene amaisunga. Anthu onse ndi opusa, alibe nzeru. Mmisiri aliyense wosula amachita manyazi ndi mafano ake. Mafano amene amapangawo ngabodza mwa iwo mulibe konse moyo. Mafanowo ngachabechabe, ayenera kuŵaseka, ndipo pamene anthuwo adzalangidwe, mafanowo adzaonongeka. Koma Iye uja amene ali choloŵa cha Yakobe sali ngati mafanowo, Iye ndiyedi Mlengi wa zonse. Aisraele ndi anthu ake amene Iye adaŵasankha, dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse. Tolatolani katundu wanu, osamsiyanso pansi, inu amene adani akuzingani ndi zithando zankhondo. Chauta akunena kuti, “Tsopano ndichotsa anthu onse a m'dziko lino. Ndidzaŵagwetsa m'mavuto, mpaka aŵamve ndithu.” Ali apa amvekere, “Kalanga ine chifukwa cha kupweteka koopsa! Bala langa ndi lomvetsa chisoni. Kale ndinkati chimenechi ndi chilango changa, ndingochipirira basi.” Hema langa laonongeka, zingwe zake zonse zaduka. Ana anga andisiya ndipo kulibenso. Palibenso wina woti nkundikhomera hema, kapena woti nkufunyulula nsalu zake. Paja abusa ndi opusa, sapempha nzeru kwa Chauta. Nchifukwa chake zinthu sizidaŵayendere bwino, ndipo nkhosa zao zidabalalika. Tamvani, kukubwera mphekesera. Kumpoto kukuchokera chinamtindi chosokosa chodzasakaza mizinda ya Yuda, kuti isanduke bwinja, mokhala nkhandwe basi. Inu Chauta, ndikudziŵa kuti moyo umene ali nawo munthu si wake. Munthu sangathe kudzitsogolera yekha. Langizeni, Inu Chauta, koma mwachilungamo. Musandikwiyire kuti mungandiwononge. Ukali wanu uyakire mitundu imene sikudziŵani, ndiye kuti anthu amene satama dzina lanu mopemba. Iwo adasakaza anthu anu ndi kuŵaononga kotheratu ndipo dziko lao adalisandutsa bwinja. Chauta adauza Yeremiya kuti, “Imva mau a chipangano ichi, ndipo ulankhule nawo anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu. Uŵauze kuti mau a Chauta, Mulungu wa Israele, ndi aŵa: Atembereredwe munthu amene sasunga mau a chipangano, chimene ndidachita ndi makolo anu, nditaŵatulutsa ku dziko la Ejipito. Nditaŵachotsa m'ng'anjo ya moto ija, ndidati, ‘Mukamandimvera ndi kumachita zimene ndikuuzani, inu mudzakhala anthu anga, Ine ndidzakhala Mulungu wanu. Choncho ndidzachita zimene ndidalonjeza makolo anu molumbira, zakuti ndidzaŵapatsa dziko lamwanaalirenji, dziko limene mukukhalamoli.’ ” Tsono ine ndidayankha kuti, “Zikhale momwemo, Inu Chauta.” Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Ulalike mau onseŵa ku mizinda ya ku Yuda ndi m'miseu ya mu Yerusalemu. Uŵauze kuti, ‘Imvani mau a chipangano ichi, ndipo muŵasunge. Nthaŵi ndi nthaŵi ndakhala ndikuŵachenjeza makolo anu kuyambira pamene ndidaŵatulutsa ku dziko la Ejipito mpaka lero lino. Ndakhala ndikuŵauza kuti, “Mverani mau anga.” Koma sadamvere, sadalabadeko. Aliyense adangoti nkhongo gwa, kutsata makhalidwe a mtima wake woipa. Ndidaŵalamula kuti asunge chipangano changa, koma iwo sadachisunge. Nchifukwa chake ndidaŵalanga monga m'mene ndidaanenera.’ ” Kenaka Chauta adandiwuza kuti, “Anthu a ku Yuda ndi anthu a mu Yerusalemu andiwukira. Abwereranso ku machimo a makolo ao amene adakana kundimvera. Akutsata milungu ina ndi kumaipembedza. A ku Israele ndi a ku Yuda aphwanya chipangano chimene ndidapangana ndi makolo ao. Nchifukwa chake Ine Chauta ndikunena kuti ndidzaŵagwetsa m'mavuto amene sangathe kuŵalewa. Ngakhale alire kwa Ine, sindidzamvera. Anthu a m'mizinda ya ku Yuda ndi a mu Yerusalemu adzapita kukalirira chithandizo kwa milungu imene ankaperekako nsembe. Koma singathe kuŵapulumutsa pa nthaŵi ya mavuto ao. Zoonadi, iwe Yuda, milungu yako yachuluka ngati chiŵerengero cha midzi yako. Maguwa ootcherapo nsembe kwa Baala achuluka ngati miseu ya mu Yerusalemu. Tsono iwe Yeremiya, usaŵapempherere anthu ameneŵa. Usaŵapepesere kwa Ine kapena kuŵadandaulira. Ndithu, Ine sindidzaŵamvera akadzandiitana pa nthaŵi ya mavuto ao. Kodi anthu anga okondedwa adzachitanji m'Nyumba mwanga? Suja iwowo achita zoipa kwambiri? Kodi malumbiro anu ndi nyama zopereka ku nsembe zingathe kukutetezani ku tsoka lanu? Kale Chauta ankakuyerekezani ndi mtengo wa olivi wa masamba obiriŵira ndi wa zipatso zokongola. Koma tsopano adzautentha ndi mkuntho wamkokomo, ndipo nthambi zake zidzapserera. Chauta Wamphamvuzonse, yemwe adakubzalani, ndiye wagamula kuti adzakulangani koopsa, chifukwa cha zoipa zimene mudachita, inu a m'banja la Israele ndi la Yuda. Mwamukwiyitsa pakupereka nsembe zopsereza kwa Baala.” Chauta adandiwululira, ndipo ndidadziŵa za chiwembu cha anthu. Iye adatsekula maso anga nandiwonetsa ntchito zao zoipa. Ndidakhala ngati mwanawankhosa amene akupita naye kokamupha. Sindidadziŵe kuti chidaloza pa ine chiwembu chimene ankakonzekera nkumanena kuti, “Tiyeni tiwudule mtengowu ukali moyo. Tiyeni timuphe munthu ameneyu, kuti asadzakumbukikenso.” Inu Chauta Wamphamvuzonse amene mumaweruza molungama, amene mumayesa mtima ndi maganizo, onetseni kuti mwaŵalipsira, pajatu ndidadzipereka m'manja mwanu! Nchifukwa chake Chauta akunena za anthu a ku Anatoti amene afuna kuwononga moyo wanga namanena kuti, “Usalosenso m'dzina la Chauta kuti tingakuphe.” Nchifukwa chake Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Ndidzaŵalanga. Anyamata ao adzaphedwa ku nkhondo. Ana ao aamuna ndi aakazi adzafa ndi njala. Sadzapulumuka ndi mmodzi yemwe, chifukwa ndidzaononga anthu a ku Anatoti, chikadzafika chaka chao cha chilango.” Inu Chauta nditati nditsutsane nanu, wokhoza ndinu ndithu. Komabe ndifuna kudandaulako kwa Inu za mlandu wanga. Chifukwa chiyani anthu oipa zinthu zimaŵayendera bwino? Chifukwa chiyani anthu osakhulupirika amakhala pabwino? Inu mudaŵabzala, ndipo adamera mizu. Amakula, namabala zipatso. Amakonda kulankhula za Inu, koma mitima yao ili kutali ndi Inu. Koma Inu Chauta ine mumandidziŵa. Mumandiyang'ana, ndipo mumayesa mtima wanga, nkuwona kuti ndimakukondani. Muŵakoke anthu oipa ngati nkhosa zokaphedwa. Muŵaike padera mpaka tsiku loti akaphedwe. Kodi dziko lidzakhala likulirabe mpaka liti? Ndipo udzu wake udzakhalabe wouma mpaka liti? Palibe mbalame kapena nyama zimene zatsala chifukwa anthu okhalamo ndi oipa kwambiri. Amati, “Mulungu sadzaona zimene zidzatiwonekere masiku athu otsiriza.” Chauta adayankha kuti, “Ngati kukutopetsa kuthamanga ndi anthu, nanga udzapikisana bwanji ndi akavalo? Ngati mtima wako ulefuka m'dziko lokoma, nanga udzatani m'nkhalango ya ku Yordani? Ngakhale abale ako ndi anansi ako nawonso amakuchita chiwembu, onsewo amvana pa zokuimba mlandu, usaŵakhulupirire, ngakhale alankhule nawe mau okoma. “Banja la Israele ndalisiya, ndaŵataya anthu amene ndidaŵasankha. Okondeka anga ndaŵapereka kwa adani ao. Anthu anga osankhidwa asanduka ngati mikango yakuthengo, amandidzumira mwaukali. Nchifukwa chake ndimadana nawo. Anthu anga osankhidwa ali ngati mbalame yamaŵangamaŵanga imene akabaŵi aizinga kuchokera konsekonse. Kasonkhanitseni nyama zakuthengo, mubwere nazo ku phwando. Abusa ambiri adaononga munda wanga wamphesa, adapondereza munda wanga. Munda wokoma uja adausandutsa chipululu. Ndithu adausandutsa chipululu, ukundilirira Ine uli wokhawokha. Dziko lonse lasanduka chipululu, ndipo palibe amene akusamalako. Anthu oononga abalalikira ku zitunda zonse zam'chipululu. Ndipo Ine Chauta ndatuma ankhondo kuti akanthe dziko lonse, kuyambira ku malire ena mpaka ku malire enanso. Palibe aliyense amene angapeze mtendere. Anthu adafesa tirigu, koma adakolola minga. Adadzitopetsa pogwira ntchito, koma osapindula nkanthu komwe. Zokolola zao nzochititsa manyazi, chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Chauta.” Chauta akuti, “Anthu oipa onse oyandikana ndi Aisraele, akulanda Aisraelowo dziko, choloŵa chimene ndidapatsa anthu angawo. Nchifukwa chake ndidzaŵachotsa m'dziko limenelo, ndipo ndidzachotsa banja la Yuda pakati pao. Komabe nditaŵachotsa, ndidzaŵamveranso chifundo, ndipo ndidzabwezanso mtundu uliwonse ku dziko la choloŵa chake. Tsono iwo akadzaphunzira bwino njira za mayendedwe a anthu anga, ndi kumalumbira m'dzina langa kuti, ‘Pali Chauta Wamoyo,’ monga momwe iwo adaphunzitsira anthu anga kumalumbira m'dzina la Baala, ndiye kuti iwowo ndidzaŵakhazikitsa pakati pa anthu anga. Komatu ngati mtundu wina uliwonse sudzamvera Ine, ndidzauwononga kotheratu.” Chauta adandiwuza kuti, “Pita ukagule mpango wa nsalu yabafuta, ukavale m'chiwuno, koma osakauviika m'madzi.” Choncho ndidakagula mpango, monga momwe Chauta adaandiwuzira, ndipo ndidauvala m'chiwuno. Chauta adandiwuzanso mau kachiŵiri kuti, “Tenga mpango uja udagula nkuvala m'chiwuno mwakowu. Unyamuke nkupita msanga ku mtsinje wa Yufurate. Kumeneko ukabise mpangowo m'ming'alu yam'mathanthwe.” Tsono ndidapitadi kukaubisa mpangowo ku Yufurate, monga momwe Chauta adaandiwuzira. Patapita masiku ambiri Chauta adandiwuza kuti, “Nyamuka, pita ku Yufurate, ukatenge mpango wam'chiwuno uja umene ndidaakuuza kuti ukaubise kumeneko.” Ine ndidapita ku Yufurate, ndipo ndidakumba pa malo amene ndidaubisa paja, nkuutenga. Koma ndidaona kuti ndi woonongeka kotheratu, wopandanso ntchito. Apo mau a adandifikanso: Chauta adandiwuza kuti, “Ndimotu m'mene ndidzaonongere zimene a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu amanyadira. Anthu oipaŵa akana kumvera mau anga. Atsata milungu ina, namaitumikira nkumaipembedza. Iwowo adzakhala ngati mpango wopanda ntchitowu. Monga mpango umakanirira m'chiwuno mwa munthu, chonchonso ndidakonza kuti banja lonse la Israele ndi la Yuda lindikangamire kuti onse akhale anthu anga, kuti adzatamande dzina langa ndi kundilemekeza. Koma iwowo sadamvere. “Ukaŵauze anthu mau amene Ine Chauta Mulungu wa Israele ndikunena, akuti: Mtsuko uliwonse wa vinyo adzaudzaza ndi vinyo. Iwowo adzakuyankha kuti, ‘Tikudziŵa bwino kuti mtsuko uliwonse wa vinyo adzaudzaza ndi vinyo.’ Tsono ukaŵauze kuti, Chauta akuti, Ndidzaŵamwetsa vinyo anthu onse am'dzikomo mpaka kuledzera. Anthuwo ndi aŵa: mafumu okhala pa mpando wa Davide, ansembe, aneneri, ndi onse okhala mu Yerusalemu. Ndidzaŵagundanitsa mitu kuti aphwanyane okhaokha, atate ndi ana ao!” Akuterotu Chauta. “Sindidzaŵachitira chifundo kapena kuŵamvera chisoni, kapena kukhululuka mtima mpaka nditaŵaononga.” Inu Aisraele, imvani ndipo tcherani khutu. Musakhale odzimva chifukwa ndi Chauta amene akulankhula. Mlemekezeni Chauta, Mulungu wanu, asanagwetse mdima, mapazi anu asanakhumudwe m'chisisira cham'mapiri, asanasandutse kuŵala, kumene mukukufuna, kuti kukhale mdima wandiweyani. Koma mukapanda kumvera, mtima wanga udzalira m'seri chifukwa cha kunyada kwanu. M'maso mwanga mudzadzaza misozi yoŵaŵa chifukwa choti nkhosa za Chauta zatengedwa ukapolo. Uza mfumu pamodzi ndi mai wake kuti, “Tsikani pa mipando yaufumu, poti zisoti zanu zokongola zaufumu zagwa pansi. Mizinda yanu ya ku Negebu aitsekera kunja, palibe wina woti nkuitsekula. Yuda yense watengedwa ukapolo, watengedwa yense ukapolo. “Ŵeramukani, inu a ku Yerusalemu, muwone adani amene akuchokera kumpoto. Kodi nkhosa zimene adakusungitsani zili kuti, nkhosa zanu zokongola zija? Kodi mudzatani akadzakuikirani kuti azikulamulirani anthu amene munkaŵayesa abwenzi anu? Kodi simudzamva zoŵaŵa zonga za mkazi pa nthaŵi yochira? Mukamadzifunsa kuti, ‘Kodi zimenezi zatigwera bwanji?’ Nchifukwa cha machimo anu ambiri kuti zovala zanu zikwinzidwe, ndipo kuti akuchiteni zankhanza. Kodi munthu wakuda nkusintha khungu lake? Kodi kambuku nkusintha maŵanga ake? Ndiye kuti inuyo, ozoloŵera kuchimwanu, mungathe kumachita zabwino ngati? Chifukwa cha kuipa kwanuko, ndidzakumwazani ngati mankhusu, onka nauluka ndi mphepo yakuchipululu. Zokuyenerani nzimenezi, chilango chimene ndakukonzerani chifukwa choti mwandiiŵala, mwakhala mukudalira milungu yonama,” akuterotu Chauta. “Ine Chauta ndidzakwinza zovala zanu mpaka kumaso, ndipo maliseche anu adzaoneka. Ndaona zonyansa zanu, zigololo zanu, kutchetcherera kwanu, ndi ziwerewere zanu zochitika pa mapiri, kuthengo. Tsoka kwa inu a ku Yerusalemu! Mudzakhala osayeretsedwabe pa zachipembedzo mpaka liti?” Ine Yeremiya Chauta adandiwuza mau onena za chilala, mau ake adati, “Yuda akulira, mizinda yake ikuvutika, anthu ake adzigwetsa pansi mwachisoni. Kulira kwa anthu a mu Yerusalemu kwakula. Atsogoleri ao otchuka akutuma antchito ao kuti akatunge madzi. Apita ku zitsime, koma osapezako madzi, ndiye akubwerera ndi mitsuko yopanda kanthu. Achita manyazi ndipo atha nzeru, adziphimba kumaso. Pansi mpouma kotheratu, poti kulibe mvula. Alimi akuchita manyazi, ndipo adziphimba kumaso. Mbaŵala yomwe ikusiya mwana wake wakhanda ku thengo chifukwa choti kulibe msipu. Mbidzi zikuima pa zitunda zopanda kanthu, zikupuma moti ŵefuŵefu ngati nkhandwe. M'maso mwachita chidima, chifukwa chosoŵa msipu.” Anthu akuti, “Inu Chauta, ngakhale machimo athu akutipalamulitsa, komabe muchitepo kanthu kuti dzina lanu lisanyozeke. Kusakhulupirika kwathu nkwakukuludi. Takuchimwirani zedi. Inu Chauta, amene muli chikhulupiriro cha Aisraele, ndiponso Mpulumutsi wao pa nthaŵi ya mavuto, mukukhaliranji ngati mlendo m'dziko lino, ngati wapaulendo wogona usiku umodzi? Chifukwa chiyani mukukhala ngati munthu wothedwa nzeru? Mukukhaliranji ngati wankhondo amene sangathenso kupulumutsa anthu? Komabe Inu Chauta, muli pakati pathu, ife amene timadziŵika ndi dzina lanu, choncho musatisiye tokha.” Chauta akunena za anthu ameneŵa kuti, “Amakonda kuyendayenda kumene afuna, ndipo sangathe kudziletsa. Nchifukwa chake Ine Chauta sindingakondwere nawo, ndipo tsopano ndidzakumbukira kuipa kwao, ndidzaŵalanga chifukwa cha machimo ao.” Pambuyo pake Chauta adandiwuza kuti, “Usaŵapempherere anthu ameneŵa, kuŵafunira zabwino. Ngakhale asale zakudya, Ine sindidzamva kulira kwao. Ndipo ngakhale apereke nsembe zopsereza ndi chopereka cha chakudya, sindidzazilandira. Koma ndidzaŵaononga ndi nkhondo, njala ndi mliri.” Koma ine ndidati, “Ha, Inu Chauta, aneneri ao amauza anthu kuti sadzafa ndi nkhondo, ndipo simudzagwa njala m'dziko mwathu, koma mudzakhala mtendere wokhawokha.” Koma Chauta adandiyankha kuti, “Zakuti aneneriwo amalosa m'dzina langa, ili ndi bodza. Ine sindidaŵasankhe, sindidaŵatume kapena kulankhula nawo. Iwo amakuloserani zinthu zonama zimene akuti adaziwona m'masomphenya. Amaombeza zabodza, zimene amalankhula ndi zonyenga zopeka iwo eni ake. Nchifukwa chake Ine Chauta ndikunena kuti aneneri ameneŵa akulosa m'dzina langa pamene sindidaŵatume. Amakuuzani kuti simudzafa pa nkhondo kapena ndi njala m'dziko lino. Koma aneneriwo ndiwo amene adzaphedwe pa nkhondo kapena kufa ndi njala. Anthu amene adaŵalosera adzaponyedwa m'miseu ya mu Yerusalemu, atafa pa nkhondo kapena ndi njala. Iwowo, akazi ao, ana ao aamuna ndi ana ao aakazi, onse adzafa, ndipo sipadzaoneka oika maliro ao. Ndithu ndidzaŵalanga poŵagwetsa m'mavuto oŵayenerera.” “Ukaŵauze kuti, ‘Maso anga adze misozi kosalekeza usiku ndi usana. Pakuti anthu anga osankhidwa ali ndi bala lalikulu, akanthidwa kwamphamvu. Ndikamayenda ku thengo, ndikuwona anthu ophedwa pa nkhondo. Ndikaloŵa mu mzinda, ndikuwona anthu ofa ndi njala. Aneneri ndi ansembe akupitirizabe ntchito zao m'dzikomo, koma osadziŵa zimene akuchita.’ ” Kodi anthu a ku Yuda mwaŵatayiratu? Kodi anthu a mu Ziyoni akuipirani m'maso? Chifukwa chiyani mwatikantha kotero kuti sitingathenso kukhala bwino? Tinkayembekeza mtendere, koma sitidaupeze. Tinkayembekeza kuchira, koma tidangoopsedwa kwambiri. Inu Chauta, tikuvomera kuipa kwathu ndiponso kupalamula kwa makolo athu. Ifeyo tidakuchimwiranidi. Musatikane, kuti dzina lanu linganyozeke. Musanyoze mpando wanu wachifumu ndi waulemerero. Mukumbukire chipangano chanu ndi ife, ndipo musachiphwanye. Pakati pa milungu yonama ya anthu a mitundu ina, kodi alipo mulungu wina amene angathe kupereka mvula? Kodi mlengalenga umapereka mvula pawokha? Kodi Inu Chauta, suja ndinu nokha amene mumachita zimenezi? Nchifukwa chake timakhulupirira Inu, popeza kuti ndinu amene mumachita zinthu zonsezi. Pambuyo pake Chauta adandiwuza kuti, “Ngakhale Mose ndi Samuele akadaima pamaso panga akupempherera anthu ameneŵa, sindikadaŵamvera chisoni. Achotseni, ndisaŵaonenso, apite basi. Akakufunsa kuti, ‘Kodi tipite kuti?’ Uŵauze kuti Ine ndati, “ ‘Oyenera mliri adzafa ndi mliri, oyenera lupanga adzafa ndi lupanga, oyenera njala adzafa ndi njala, oyenera ukapolo, adzapita ku ukapolo.’ “Ndidzaŵagwetsera zinthu zinai izi zoŵaononga: lupanga loŵapha, agalu oŵaluma, mbalame zamumlengalenga ndiponso zilombo zoti ziŵaphe ndi kuŵadya. Ndidzaŵasandutsa chinthu chochititsa nyansi kwa anthu a m'maufumu onse a dziko lapansi, chifukwa cha zimene Manase mwana wa Hezekiya, mfumu ya ku Yuda, adachita ku Yerusalemu.” Chauta akuti, “Kodi inu a ku Yerusalemu adzakumverani chisoni ndani? Adzakulirani ndani? Ndani adzapatuke kuti akufunseni za moyo wanu? Ine mudandikana, mukupitirirabe kundifulatira. Motero ndidakweza mkono wanga nkukukanthani. Ndidatopa nako kukhululuka. Ndidaŵabalalitsira uku ndi uku, monga momwe amachitira ndi mankhusu popeta ndi lichero. Ndidaŵaliritsa anthu anga ndi kuŵaononga, chifukwa sadafune kusiya makhalidwe ao oipa. Akazi amasiye ndidaŵachulukitsa, kupambana mchenga wakunyanja. Amai ndidaŵaonongera ana ao akali anyamata abiriŵiri. Mwadzidzidzi ndidaŵagwetsera chisoni ndi nkhaŵa. Mai wa ana asanu ndi aŵiri wakomoka, akupuma mwabefu. Mdima wamgwera kukadali masana. Adamchititsa manyazi ndipo wataya mtima. Otsala onse ndidzaŵapereka kwa adani kuti aŵaphe ndi lupanga,” akuterotu Chauta. Inu mai wanga, tsoka kwa ine kuti mudandibala ine munthu wokangana ndi wotsutsana ndi anthu pa dziko lonse. Sindidakongole kanthu kwa munthu kapena kukongoza munthu kanthu. Komabe anthu onse akunditukwana. Chauta adayankha kuti, “Koma zoonadi ndidzakulanditsa kuti upeze bwino. Ndithudi, adani ako adzakupemba pa nthaŵi ya tsoka ndi ya mavuto. Kodi munthu angathe kudula chitsulo, chitsulo chochokera kumpoto chosakaniza ndi mkuŵa? “Anthu inu, chuma chanu chonse pamodzi ndi katundu wanu ndidzazipereka kwa ofunkha popanda malipiro, chifukwa cha machimo anu ambiri m'dziko lonse. Ndidzakusandutsani akapolo a adani anu m'dziko limene simulidziŵa. Ndithudi, mkwiyo wanga wayaka, ndipo udzakutenthani kosalekeza.” Ine ndidati, “Inu Chauta, mumadziŵa zonse. Mundikumbukire ndipo mundithandize. Mundilipsirire anthu ondizunza. Mundilezere mtima, musandilande moyo. Onani mavuto amene ndikupeza chifukwa cha Inu. Nditamva mau anu, ndidaŵalandira bwino, mauwo adandipatsa chimwemwe ndi chisangalalo. Paja Inu Chauta Wamphamvuzonse, ndimadziŵika ndi dzina lanu. Sindidakhale nao m'gulu la anthu amadyera, sindidasangalale nawo anthu amenewo. Ndidakhala ndekha chifukwa choti dzanja lanu linali pa ine, ndipo mumtima mwanga mudadzaza mkwiyo. Nanga chifukwa chiyani mavuto anga sakutha? Chilonda changa nchosatha, sichikupola. Monga nkuti mwandinyenga ngati chitsime chouma kapena ngati mtsinje wopanda madzi?” Chauta adayankha kuti, “Ukabwerera kwa Ine, ndidzakulandiranso, ndipo udzanditumikiranso. Ukamalankhula zenizeni, osati zachabe, udzakhala wondilankhulira. Anthu ameneŵa ayenera kudzabweranso kwa iwe, koma iwe usabwerere kwa iwowo. Ndidzakusandutsa wolimba ngati linga lamkuŵa kwa anthuwo. Iwo adzalimbana nawe, koma sadzakupambana, pakuti Ine ndili nawe, ndidzakulanditsa ndi kukupulumutsa. Ndidzakulanditsa kwa anthu oipa, ndipo ndidzakuwombola kwa anthu ankhanza,” akuterotu Chauta. Chauta adandiwuza kuti, “Usadzakwatire, usadzabale ana aamuna kapena aakazi ku malo ano. Ndithu kunena za ana aamuna kapena ana aakazi obadwira kuno, kapenanso za amai ao ndi atate ao amene adabereka anawo m'dziko muno, onsewo adzafa ndi nthenda zoopsa. Sadzaŵalira maliro kapena kuŵaika m'manda. Adzakhala ngati ndoŵe yotayikira pansi. Ena adzafera pa nkhondo, ena adzafa ndi njala. Ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame ndi zilombo zakuthengo.” Chauta akunena kuti, “Usaloŵe m'nyumba ya maliro. Usaloŵemo kuti ukalire kapena kutonthoza anthu, pakuti ndaŵachotsera mtendere wanga. Ndachotsanso chikondi changa chosasinthika ndiponso chifundo changa. Akuluakulu ndi ang'onoang'ono omwe, onsewo adzafa m'dziko lino. Koma maliro ao sadzaikidwa, iwowo sadzaŵalira. Palibe amene adzaonetse chisoni podzichekacheka kapena kumeta tsitsi chifukwa cha malirowo. Palibe amene adzapatse chakudya munthu wolira kuti amtonthoze chifukwa cha akufawo. Sadzamupatsa chakumwa kuti amtonthoze, ngakhale amwalire atate ake kapena amai ake. “Usadzaloŵe m'nyumba m'mene muli phwando, kuti udye nao ndi kumwa nao,” Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, “Pa nthaŵi yanu yomwe, ndiponso pa malo omwe ano ndidzathetsa mau achisangalalo ndi achimwemwe, ndipo ndidzachotsa liwu la mkwati wamwamuna ndi la mkwati wamkazi inuyo mukuwona. “Tsono ukadzaŵauza anthuwo mau ameneŵa, makamaka adzakufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani Chauta wanena kuti tsoka lotere lidzatigwera ifeyo? Kodi tidalakwanji? Kodi Inu Chauta, Mulungu wathu, takuchimwirani chiyani?’ Tsono iwe udzayankhe kuti, ‘Nchifukwa chakuti makolo anu adandisiya Ine,’ akuterotu Chauta. ‘Adatsata milungu ina, namaitumikira ndi kumaipembedza. Adandisiya Ine, ndipo sadamvere malamulo anga. Komanso inu mudachimwa koposa kupambana makolo anu: aliyense mwa inu akutsata zoipa ndi mtima wake wokanika, m'malo momandimvera Ine. Motero Ine ndidzakupirikitsani m'dziko lino ndi kukuloŵetsani m'dziko limene inu ndi makolo anu simulidziŵa. Kumeneko mudzatumikira milungu ina usana ndi usiku, chifukwa Ine sindidzakuchitiraninso chifundo.’ ” Nchifukwa chake Chauta akunena kuti, “Masiku akubwera pamene anthu polumbira sazidzatinso, ‘Pali Chauta wamoyo, amene adatulutsa Aisraele ku dziko la Ejipito!’ Koma azidzati, ‘Pali Chauta wamoyo, amene adatulutsa Aisraele ku dziko lakumpoto, ndi ku maiko konse kumene adaŵabalalitsira!’ Ndithu ndidzaŵabwezera ku malo amene ndidapatsa makolo ao.” Chauta akuti, “Ndidzaitana adani ambiri okhala ngati asodzi a nsomba, ndipo adzaŵagwira anthuŵa ngati nsomba. Pambuyo pake ndidzaitana adani enanso ambiri okhala ngati alenje, kuti akaŵasake anthuŵa ku mapiri, ku zitunda, ndiponso m'mapanga am'matanthwe. Maso anga amaona makhalidwe ao onse oipa, ndi osabisika pamaso panga. Palibenso tchimo lililonse limene sindikulidziŵa. Ndidzaŵalanga moŵirikiza, chifukwa cha kuipa kwao ndi machimo ao. Ndidzatero chifukwa chakuti aipitsa dziko langa ndi mafano ao amene ali ngati mitembo, ndipo dziko limene lili choloŵa changa adalidzaza ndi mafano ao onyansa.” Inu Chauta, ndinu mphamvu zanga ndi linga langa, ndinu pothaŵira panga pa nthaŵi ya mavuto. Anthu a mitundu yonse adzabwera kwa Inu kuchokera ku malire onse a dziko lapansi. Adzati, “Makolo athu anali ndi milungu yonama, anali ndi mafano achabechabe opanda phindu. Kodi munthu nkudzipangira milungu yeniyeni? Atati apange, singakhale milungu konse.” Chauta akuti, “Nchifukwa chake ndidzaŵaphunzitsa, ndidzaŵaphunzitsa kokha kano kuti adziŵe mphamvu zanga zopambana. Ndithudi adzadziŵa kuti Ine dzina langa ndine Chauta.” Chauta akuti, “Uchimo wa Yuda ndi wolembedwa ndi cholembera chachitsulo, cha nsonga ya mwala wadaimondi. Uchimowo walembedwa pa mitima yao ndiponso pa maguwa ao. Chonsecho ana ao amakumbukira maguwa ao aja ndi zoimiritsa zao zansembe, patsinde pa mtengo wogudira uliwonse, pa mapiri am'dzikomo. Chuma chanu ndi katundu wanu yense ndidzazipereka kwa ofunkha, kuti zikhale dipo la machimo anu ochitika m'dziko lanu lonse. Mudzataya dziko limene ndidakupatsani kuti likhale ngati choloŵa chanu. Ndidzakusandutsani akapolo otumikira adani anu m'dziko limene simulidziŵa. Ndithu mkwiyo wanga uli ngati moto woyaka, ndipo udzayakadi mpaka muyaya.” Chauta akunena kuti, “Tsoka kwa munthu wodalira munthu mnzake, amene amagonera pa munthu mnzake kuti amthandize, pamene mtima wake wafulatira Chauta. Woteroyo adzakhala ngati chitsamba m'chipululu, ndipo sadzapeza zabwino. Adzakhala m'chipululu mopanda madzi, m'dziko lamchere m'mene anthu sangathe kukhalamo. “Koma ndi wodala munthu wokhulupirira Chauta, amene amagonera pa Chautayo. Adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m'mphepete mwa mtsinje, umene umatambalitsa mizu yake m'mbali mwa madzi. Suwopa kukamatentha, chifukwa masamba ake safota. Pa chaka chachilala sukuda nkhaŵa, ndipo suleka kubala zipatso.” Mtima wa munthu ndi chinthu chonyenga kwambiri kupambana zinthu zonse. Kuipa kwake nkosachizika. Kodi ndani angathe kuumvetsa? “Koma Ine Chauta ndimafufuza maganizo ndi kuuyesa mtimawo. Ndimamchitira munthu aliyense molingana ndi makhalidwe ake ndiponso moyenerera ntchito zake.” Munthu wopeza chuma pobera anthu ena, ali ngati nkhwali yokonkhomola mazira amene sidaikire. Masiku asanachuluke, chumacho chimamthera, potsiriza amasanduka ngati chitsilu. Nyumba yathu yopembedzeramo ili ngati mpando waufumu waulemerero, wokhazikika pa phiri lalitali chiyambire. Inu Chauta, amene Aisraele amagonera pa Inu, onse okukanani adzaŵachititsa manyazi. Onse okusiyani adzafafanizika ngati maina olembedwa pa dothi, chifukwa chokana Chauta, kasupe wa madzi opatsa moyo. Inu Chauta, chiritseni ndipo ndidzachiradi. Pulumutseni ndipo ndidzapulumukadi. Ndinu amene ndimakutamandani. Anthu akundifunsa kuti, “Zija ankanena Chautazi zili kuti? Zitachitikatu kuti tiziwone!” Ine sindidakukakamizeni kuti mufikitse zovuta. Mukudziŵa kuti tsiku la tsoka sindinkalilakalaka. Zonse zimene ndidalankhula mukuzidziŵa. Musandichititse mantha. Inu nokha ndiye pothaŵira panga, tsoka likandigwera. Koma ondizunza ndiwo achite manyazi, osati ineyo. Ade nkhaŵa ndi iwowo, osati ineyo. Tsiku la tsoka liŵafikire, ndipo muŵaononge kotheratu. Chauta adandiwuza kuti, “Pita ukaime pa chipata chachikulu chodzerapo anthu ambiri, chimene mafumu a ku Yuda amaloŵerapo ndi kutulukirapo. Upitenso ku zipata zonse za Yerusalemu. Ukanene kuti: Imvani mau a Chauta, inu mafumu a ku Yuda, inu anthu a ku Yuda, ndi inu nonse okhala mu Yerusalemu amene mumaloŵera pa zipata zimenezi. M'mau a Chautawo ndi aŵa: Kuti musunge moyo wanu, samalani bwino kuti pa tsiku la Sabata musanyamule katundu, kapena kuloŵa naye pa zipata za Yerusalemu. Musanyamule katundu aliyense kutuluka naye m'nyumba mwanu, kapena kugwira ntchito iliyonse pa Sabata. Koma muzilisunga tsiku la Sabatalo kuti likhale lopatulika, monga ndidalamulira makolo anu. Iwowo sadamvere kapena kusamalako, koma ndi mitima yokanika adakana kumva ndi kulandira malangizo anga.” Tsono Chauta akunena kuti, “Koma inu muzindimvera Ine, ndi kuleka kunyamula katundu kapena kumatuluka naye pa zipata za mzinda uno pa Sabata, ndipo muzisunga tsiku la Sabata osagwira ntchito pa tsiku limenelo. Mukatsata zimenezi, ndiye kuti pa zipata za mzinda umenewu pazidzaloŵera mafumu odzakhala pa mpando waufumu wa Davide. Azidzaloŵa atakwera pa magareta ndi pa akavalo, ali pamodzi ndi akalonga ao ndi anthu a ku Yuda ndiponso anthu a mu Yerusalemu. Ndipo anthu adzakhazikika mu mzinda umenewu mpaka muyaya. Anthu adzachokera ku mizinda ya Yuda ndi dziko lonse lozungulira Yerusalemu, dziko la Benjamini, dziko lazidikha, dziko lazitunda, ndiponso ku Negebu, atatenga nsembe zopsereza, nsembe zaufa, nsembe zalubani, ndiponso nsembe zothokozera, kupita nazo ku Nyumba ya Chauta. Koma inu mukapanda kundimvera, mukapanda kusunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika, ndipo mukamanyamula katundu aliyense nkumakaloŵa pa zipata za Yerusalemu pa tsiku la Sabata, ndiye kuti ndidzazitentha zipata zimenezo. Moto udzapsereza nyumba zaufumu za ku Yerusalemu, moto wake wosazimika.” Chauta adauza Yeremiya kuti, “Nyamuka, upite ku nyumba ya munthu woumba mbiya, kumeneko ukamva mau anga.” Motero ndidatsikira ku nyumba ya woumba mbiya, ndipo ndidampeza akuumba mbiya pa mkombero. Chiŵiya chimene ankaumbacho chitakhala chopotoka pomalinga ndi kaumbidwe kake kolakwika, iye uja ankaumbanso chiŵiya china ndi dothi lomwelo, monga ankafunira mwiniwakeyo. Tsono Chauta adafunsa kuti. “Inu Aisraele, kodi Ine sindingathe kuchita nanu monga amachitira woumba mbiya? Zedi, inuyo muli m'manja mwangamu monga momwe umakhalira mtapo m'manja mwa woumba mbiya. Ngati ndichenjeza mtundu wa anthu kapena ufumu kuti ndidzaugwetsa ndi kuuwononga, ngati mtundu umene ndauchenjezawo uleka machimo ake, ndiye kuti sindidzaulanga monga m'mene ndinkaganizira. Momwemonso ngati ndifuna kuyambitsa ndi kukhazikitsa mtundu kapena ufumu wina, koma mtunduwo nkumapitiriza kuchita zoipa pamaso panga, osamvera mau anga, ndiye kuti sindidzauchitira zabwino zimene ndidaati ndiwuchitire. Pita tsono, ukauze anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti Chauta akuti, Ine ndikukonzekera zoti ndikuchiteni, ndikuganiza zoti ndikulangeni. Bwererani nonse, aliyense aleke njira zake zoipa. Konzani makhalidwe anu ndi zochita zanu. “Koma iwo adzayankha kuti, ‘Zimenezo nzopanda pake. Tidzachita monga m'mene tifunira, ndipo aliyense mwa ife azidzangotsata zoipa za mtima wake wokanika.’ ” Nchifukwa chake Chauta akunena kuti, “Ukafunse anthu a mitundu ina yonse, ngati alipo amene adamvapo zotere. Israele amene adaali ngati namwali wosadziŵa mwamuna wachita chinthu choipa kwambiri. Kodi chisanu chimatha pa mathanthwe otsetsereka a phiri la Lebanoni? Kodi mitsinje ya madzi ozizira ochokera ku phiri la Lebanoni imaphwa? Ai, komabe anthu anga andiiŵala. Amafukizira lubani mafano opanda pake. Amakhumudwa m'njira zao zakale. Amayenda m'njira zodzera m'thengo, kusiya mseu wabwino. Dziko lao amalisandutsa lochititsa nyansi ndi lodzetsa mfuu wa mantha mpaka muyaya. Aliyense wodutsamo adzakhala akudabwa ndi kumapukusa mutu. Ndidzaŵabalalitsa ngati mphepo yakuvuma. Adzathaŵa pamene adani ao akufika. Ndidzaŵafulatira osaŵathandiza pa nthaŵi ya mavuto ao.” Anthu ena adati, “Tiyeni tsono tipangane zoti timchite Yeremiya. Ansembe otitsogolera tidzakhala nawobe. Tidzakhala nawo ndithu anzeru otilangiza, ndiponso aneneri otilalikira mau a Mulungu. Tiyeni tipeze zifukwa zomuimbira mlandu, ndipo mau ake tisaŵasamale konse.” Apo ndidapemphera kwa Mulungu kuti, “Inu Chauta, mundimvere, mumve zimene adani anga akunena za ine. Kodi choipa chingakhale dipo la chinthu chabwino? Komabe andikumbira dzenje. Kumbukirani kuti paja ndidaabwera kwa Inu kudzaŵapempherera kuti muleke kuŵakwiyira. Nchifukwa chake mulange ana ao ndi njala. Muŵaononge ndi nkhondo. Akazi ao akhale amasiye, opanda ana. Amuna ao afe ndi mliri, anyamata ao afe ndi lupanga ku nkhondo. Muŵatumire gulu lankhondo lidzaŵakanthe modzidzimutsa, ndipo kulira kwamantha kumveke m'nyumba zao. Iwotu andikumbira dzenje loti andiponyemo, ndipo atchera mapazi anga msampha. Inu Chauta, mukudziŵadi ziwembu zao zonse zofuna kundipha. Musaŵakhululukire zolakwa zao, ndithu, musaŵachotsere machimo ao. Agonjetsedwe pamaso panu, ndipo muŵalange muli okwiya.” Chauta adandiwuza kuti, “Pita ukagule mtsuko wadothi kwa munthu woumba. Utenge akuluakulu ena, ndiponso ansembe ena okhwimapo. Mupite ku Chigwa cha Benihinomu, pafupi pa Chipata cha Mapale. Kumeneko ukalengeze zimene ndikukuuza tsopano. Ukanene kuti, Inu mafumu a ku Yuda ndi onse okhala ku Yerusalemu, imvani mau a Chauta. Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akuti, ‘Ndidzagwetsa tsoka loopsa pa malo ano, kotero kuti aliyense amene adzamve adzadzidzimuka kwambiri. Anthu andikana Ine, ndipo aipitsa malo ano. Akhala akufukiza lubani kwa milungu yachilendo imene iwowo, makolo ao ndiponso mafumu a ku Yuda sadaidziŵe. Ndipo pa malo ano adakhetserapo magazi a anthu osachimwa. Adamanga nsanja yopembedzerapo Baala, pamene amaperekapo ana ao kuti akhale nsembe zopsereza kwa Baala. Zimenezo sindidalamule konse, sindidazilankhule, ngakhale kuziganiza komwe. Nchifukwa chake nthaŵi ikubwera pamene malo ano sadzatchedwanso Tofeti, kapena Chigwa cha Benihinomu, koma Chigwa cha Chipheiphe. Pamalo pano ndidzasokoneza maganizo a anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu. Anthu am'menemo ndidzaŵaphetsa kwa adani ao ku nkhondo, ndipo ndidzaŵakanthitsa kwa anthu oŵazonda. Mitembo yao ndidzaisandutsa chakudya cha mbalame zamumlengalenga ndi zilombo za pa dziko lapansi. Mzinda umenewu ndidzausandutsa malo ochititsa nyansi ndiponso odzetsa mfuu wa mantha. Aliyense wodutsapo adzachita nawodi nyansi ndipo adzafuula ndi mantha poona kukanthidwa kwake. Ndidzaumiriza anthuwo kuti adye ana ao omwe aamuna ndi aakazi. Adzadyana choncho pa nthaŵi yoopsa pamene adzazingidwa ndi adani ao ofuna kuŵazunza.’ “Tsono iweyo udzaphwanye mtsuko uja, anthu amene udzapite nawowo akuwona. Ndiye udzaŵauze kuti, Chauta Wamphamvuzonse akuti, Umu ndi m'mene ndidzaonongere anthu ameneŵa, monga momwe woumba amaphwanyira mbiya yake, kotero kuti sangathenso kuikonza. Anthu akufawo adzaŵaika ku Tofeti, chifukwa choti kwina kulikonse sikudzakhala malo oŵaika. Umu ndimo m'mene ndidzaŵachitire malo ano pamodzi ndi anthu ake omwe. Mzindawu ndidzausandutsa ngati Tofeti. Nyumba za ku Yerusalemu ndi za mafumu a ku Yuda ndidzazisandutsa ngati za ku Tofeti, chifukwa ndizo nyumba zimene pa madenga ao ankaotcherapo nsembe kwa milungu ya mumlengalenga, namapereka nsembe yazakumwa kwa milungu ina.” Pambuyo pake Yeremiya adabwerako ku Tofeti kumene Chauta adaamtuma kuti akalose, naimirira m'bwalo la Nyumba ya Chauta. Ndipo adauza anthu onse kuti, “Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, Ndidzagwetsa tsoka pa mzinda uwu pamodzi ndi pa midzi yake yonse monga ndidaanenera, chifukwa choti anthu ake ndi okanika, ndipo akukana kumvera mau anga.” Wansembe Pasuri, mwana wa Imeri, amene anali kapitao wamkulu ku Nyumba ya Chauta, adamva Yeremiya akulosa zinthu zimenezi. Tsono Pasuri adalamula kuti anthu amenye mneneri Yeremiya ndi kumuika m'ndende ku chipata cha Benjamini, ku Nyumba ya Chauta. M'maŵa mwake Pasuri adatulutsa Yeremiya m'ndende, ndipo Yeremiya adauza Pasuri kuti, “Chauta sakutchulanso dzina loti Pasuri, koma loti ‘Zoopsa pa mbali zonse.’ Paja Chauta akunena kuti: Ndidzakusandutsa choopsa kwa mwiniwakewe, ndiponso kwa abwenzi ako onse. Abwenzi akowo adani ao adzaŵapha ndi lupanga, iweyo ukupenya. Ndipo Yuda yense ndidzampereka kwa mfumu ya ku Babiloni. Ena adzaŵatenga ukapolo kupita nawo ku Babiloni, ndipo ena adzaŵapha ndi lupanga. Chuma chonse chamumzindamu, phindu lonse la ntchito yake, zinthu zonse za mtengo wapatali ndi chuma cha mafumu a ku Yuda, zonsezo ndidzazipereka kwa adani ao. Iwowo adzafunkha zimenezi ndi kupita nazo ku Babiloni. Ndipo iwe Pasuri ndi onse a pabanja pako, nanunso adzakutengani ukapolo kupita nanu ku Babiloni. Mudzafera komweko ndi kuikidwa komweko, iweyo pamodzi ndi abwenzi ako amene unkaŵalosera zabodza.” Inu Chauta, mwandipusitsa ine, ndipo ndapusadi. Inu ndinu amphamvu kuposa ine, ndipo mwandipambana. Aliyense akundiseka tsiku lonse, aliyense akundinyodola kosalekeza. Ndikamalankhula, ndimakweza mau, ndimafuula kuti, “Ndeu kuno, taonongeka!” Mau anu, Inu Chauta, andisandutsa wonyozeka ndi wonyodoledwa masiku onse. Ndikanena kuti, “Sindidzalalikanso za Chauta, sindidzalankhulanso m'dzina lake,” mau anu, Inu Chauta, amayaka ngati moto mumtima mwanga. Ndimayesa kuŵasunga m'kati, koma pambuyo pake ndimaŵatulutsa popeza kuti sindingathe kupirira. Ndimamva ambiri akunong'ona. Zoopsa zili pa mbali zonse! Amati, “Kamnenezeni! Tiyeni tikamneneze!” Amene adaali abwenzi anga amayembekeza kuti ndigwa pansi, amati, “Mwina mwake adzatha kunyengedwa, tsono ife tidzamgwira ndi kulipsira pa iyeyo.” Koma Chauta ali nane, ndiye wankhondo woopsa. Nchifukwa chake anthu ondizunza adzakhumudwa, ndithu sadzandipambana. Adzachita manyazi kwambiri, chifukwa cha kundilepherako, ndipo manyazi aowo sadzaiŵalika konse. Inu Chauta Wamphamvuzonse, amene mumaweruza anthu molungama, amene mumapenya zamumtima, ndikupereka mlandu wanga kwa Inu. Ndikukupemphani kuti mundilipsirire adani anga. Imbirani Chauta, mtamandeni Chauta! Ndiye amapulumutsa osauka kwa adani ao. Litembereredwe tsiku limene ndidabadwa. Lisatamandidwe tsiku limene mai wanga adandibala. Tsoka kwa iye amene adakasangalatsa bambo wanga ndi uthenga woti, “Kunyumba kwanu kwabadwa mwana wamwamuna.” Munthu ameneyo akhale ngati mizinda imene adaiwononga Chauta mopanda chifundo ija. Amve kulira kwa kupweteka m'maŵa, ndiponso phokoso la nkhondo masana, chifukwa choti sadandiphere m'mimba, kuti mai wanga asanduke manda anga, ndipo kuti mimba yake ikhale chitupire. Kodi chifukwa chiyani ndidabadwa? Kodi ndidabadwira mavuto ndi chisoni, kuti moyo wanga ukhale wa manyazi okhaokha? Zedekiya, mfumu ya ku Yuda, adatuma Pasuri mwana wa Malakiya, ndiponso wansembe Zefaniya mwana wa Maseiya, naŵauza kuti, “Pitani kwa Yeremiya mukampemphe kuti atinenere kwa Chauta, popeza kuti Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni akufuna kutithira nkhondo. Mwina mwake Chauta nkutichitira zodabwitsa, kuti Nebukadinezara achoke kwathu kuno.” Koma otumidwa aja atafika, Yeremiya adaŵauza kuti, “Mukamuuze Zedekiya kuti Chauta, Mulungu wa Israele akuti, ‘Ndidzakulandani zida zankhondo zimene zili m'manja mwanuzo, zimene mukumenya nazo nkhondo ndi mfumu ya ku Babiloni ndi ankhondo ake amene akuzingani ndi zithando zankhondo. Ndidzabwera nazo ndi kuziika m'kati mwa mzinda uno. Ineyo mwiniwakene ndi mkono wanga wamphamvu, ndidzamenyana nanu nkhondo inuyo, ndili wopsa mtima, wokalipa ndi wokwiya. Ndidzakantha okhala mumzindamu ndi ziŵeto zomwe, ndipo zonse zidzafa ndi mliri woopsa. Pambuyo pake ndidzapititsa ku ukapolo Zedekiya mfumu ya ku Yuda pamodzi ndi nduna zake, ndi anthu otsala mumzindamu opulumuka ku mliri, ku njala ndi ku nkhondo. Ndidzaŵapereka kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndiponso kwa adani ao amene akufuna kuŵapha. Adzaŵaphadi ndi lupanga, sadzaŵamvera chisoni kapena chifundo.’ ” Chauta akunena kuti, “Anthu ameneŵa udzaŵauzenso kuti asankhulepo: kodi afuna moyo kapena imfa? Aliyense wotsala mu mzinda uno adzafa ndi nkhondo, njala kapena mliri. Koma aliyense amene adzadzipereka kwa Ababiloni amene akuzingani ndi zithando zankhondo aja, ameneyo adzakhala ndi moyo, adzapulumuka. Mzinda umenewu ndatsimikiza kuti ndidzauchita zoipa osati zabwino ai. Udzaperekedwa kwa mfumu ya ku Babiloni ndipo iyeyo adzautentha ndi moto.” “Tsono banja laufumu la ku Yuda uliwuze kuti, ‘Imvani mau a Chauta. Inu a m'banja la Davide, Chauta akunena kuti: “ ‘Muziweruza motsata chilungamo m'maŵa mulimonse, ndipo muzipulumutsa kwa anthu ozunza, aliyense amene katundu wake wabedwa, kuwopa kuti mkwiyo wanga ungayake nkukhala wosazimika, chifukwa cha machimo anu. “ ‘Ndikukuimbani mlandu, inu anthu okhala m'chigwa inu okhala ngati thanthwe lapachidikha,’ ” akutero Chauta. “Inu amene mumati, ‘Ndani angatithire nkhondo? Ndani angathe kuloŵa m'malinga mwathu?’ Ndidzakulangani potsata ntchito zanu. Ndidzatentha nkhalango yanu, moto udzapsereza zonse zimene zakuzungulirani,” akuterotu Chauta. Chauta adandiwuza kuti, “Pita ku nyumba ya mfumu ya ku Yuda, ukaiwuze kuti, ‘Iwe mfumu ya ku Yuda, imva mau a Chauta. Imva iwe amene umakhala pa mpando waufumu wa Davide, iweyo pamodzi ndi atumiki ako ndiponso anthu ako amene amaloŵera pa zipata izi. Chautatu akuti uziweruza molungama ndi mosakondera. Munthu amene adambera zake uzimpulumutsa kwa womsautsa. Usavutitse mlendo, mwana wamasiye kapena mkazi wamasiye. Usakhetse magazi a anthu osachimwa pa malo ano. Ndithu, ukamadzamvera mau aŵa, ndiye kuti mafumu okhala pa mpando waufumu wa Davide adzapitirirabe kumalamulira. Azidzaloŵera pa zipata izi za ku nyumba ya mfumu, atakwera pa magaleta ndi pa akavalo, iwowo pamodzi ndi atumiki ao ndi anthu ao. Koma ngati sudzamvera mau anga, ndikulumbira pali Ine ndemwe, kuti nyumba imeneyi idzasanduka bwinja!’ ” Akuterotu Chauta. Naŵa mau a Chauta onena za nyumba ya mfumu ya ku Yuda: “Ngakhale iwe ndimakukonda ngati Giliyadi, kapena ngati nsonga ya phiri la Lebanoni, komabe ndidzakusandutsa chipululu, mzinda wopanda anthu. Ndidzatuma anthu oti adzakuwononge, aliyense ali ndi zida zake. Adzadula mikungudza yako yokoma, nadzaiponya pa moto. “Pamene anthu a mitundu ina adzadutse pa mzinda umenewu, azidzafunsana kuti, ‘Kodi chifukwa chiyani Chauta adaononga chotere mzinda waukuluwu?’ Yankho lake lidzakhala lakuti, ‘Nchifukwa chakuti anthu akewo adasiya chipangano chimene adapangana ndi Chauta, Mulungu wao. Adayamba kupembedza milungu ina ndi kumaitumikira.’ ” Musailire mfumu, musaŵaimbire nyimbo malemuwo. Koma mulire amene wachotsedwa m'dziko lake chifukwa sadzabwereranso, sadzaliwonanso dziko lake. Paja Salumu, mwana wa Yosiya, mfumu ya ku Yuda, adaloŵa m'malo mwa atate ake pa mpando waufumu umene adausiya. Tsono ponena za amene uja Chauta akuti, “Iyeyo sadzabwereranso. Adzafera ku dziko laukapolo, ndipo sadzaliwonanso dziko lino.” “Tsoka kwa munthu womanga nyumba yake mopanda chilungamo, womanga zipinda zake monyenga, pogwiritsa ntchito anthu, koma osaŵapatsa malipiro a ntchito yao. Munthuyo amanena kuti, ‘Ndidzadzimangira nyumba yaikulu, ya zipinda zam'mwamba zikuluzikulu, ndidzaikamo mawindo, ndi kukhomamo matabwa a mkungudza, ndipo ndidzaipaka utoto wofiira.’ Kodi uganiza kuti ndiwe mfumu poti nyumba zako ndi zamkungudza? Ganiza za bambo wako: suja anali nazo zosoŵeka zonse? Suja ankaweruza molungama ndi mosakondera? Ndipo paja zonse zidamuyendera bwino. Ankateteza anthu otsika ndi osauka, ndipo zonse zinkamuyendera bwino. Kodi zimenezi sizidaonetse kuti ankandidziŵa?” Akuterotu Chauta. “Koma iwe maganizo ako ndi mtima wako sizili penanso, zili pa phindu lonyenga, pa zopha anthu osalakwa, ndi pa zankhanza ndi zozunza ena.” Nchifukwa chake Chauta ponena za Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya ku Yuda, akuti, “Sipadzakhala womulira munthu ameneyo kuti, ‘Kalanga ine, mbale wanga!’ Kapena kuti, ‘Kalanga ine, mlongo wanga!’ Sipadzakhala womulira kuti, ‘Kalanga ine, mbuye wanga!’ Kapena kuti, ‘Kalanga ine, mfumu yanga.’ Adzamuika ngati bulu basi, kuchita kumguguza nkukamtaya kuseri kwa zipata za Yerusalemu.” “Tsono inu anthu a ku Yerusalemu, kwerani ku mapiri ku Lebanoni, mukalire mofuula kumeneko, mau anu amveke mpaka ku Basani. Mulire mofuula muli ku Abarimu, chifukwa onse amene munkaŵadalira aonongeka. Ndidaakuchenjezani pamene zinthu zinkakuyenderani bwino. Koma inu mudati, ‘Sitidzamvera.’ Ndi m'mene mwakhala mukuchitira kuyambira muli ana aang'ono, simudamvere mau anga. Mphepo idzakuchotserani abusa anu onse, ndipo amene munkaŵadalira adzatengedwa ukapolo. Tsono mudzanyozedwa, mudzachita manyazi, chifukwa cha zolakwa zanu zochuluka. Inu amene mumakhala ku nyumba ya ku Lebanoni ija, amene mudamanga nyumba zanu pakati pa mikungudza, mudzalira kwambiri pamene zoŵaŵa zidzakugwerani, zonga za mkazi pa nthaŵi yake yochira.” Chauta akuti, “Pali Ine ndemwe, iwe Yehoyakini, mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda, ngakhale ukadakhala ngati mphete ya ku dzanja langa lamanja, ndikadakuvula nkukutaya. Ndidzakupereka kwa anthu ofuna kukupha, amene umaŵaopa, ndiye kuti kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni ndi anthu ake. Ndidzakupititsa ku dziko lina pamodzi ndi mai wako amene adakubala. Simudabadwire kumeneko, komabe nonsenu mudzafera kumeneko. Simudzabwereranso kudziko kumene mudzafuna kubwerera.” Ine ndidati, “Kodi ndiye kuti Yehoyakiniyu wakhala ngati mbiya yonyozeka, yosweka, chinthu chimene anthu sakuchisamala? Nanga chifukwa chiyani iyeyu ndi ana ake akuŵachotsa ndi kuŵaponya ku dziko losadziŵika konse?” Iwe dziko, iwe dziko, iwe dziko, imva mau a Chauta. Chauta akuti, “Munthu ameneyu mumtenge ngati wopanda ana, munthu amene sadzakhoza pa moyo wake. Ndithu, palibe ndi mmodzi yemwe mwa zidzukulu zake amene adzakhale pa mpando waufumu wa Davide ndi kudzalamuliranso Yuda.” “Tsoka kwa abusa amene amaononga ndi kumwaza nkhosa za pabusa panga,” akutero Chauta. Nchifukwa chake Chauta, Mulungu wa Israele, ponena za abusa oyang'anira anthu ake, akuti, “Mwabalalitsa ndi kumwaza nkhosa zanga, simudazisamale bwino. Choncho ndidzakulangani chifukwa cha machimo anu. Pambuyo pake Mwiniwakene ndidzasonkhanitsa nkhosa zanga zotsala, kuzichotsa ku malo onse amene ndidazimwazira. Ndidzazibwezera ku busa lakwao, ndipo zidzaswana ndi kuchuluka. Ndidzazipatsa abusa oziŵeta bwino. Sizidzaopanso kapena kuchita mantha, kapena kusokera,” akuterotu Chauta. Chauta akunena kuti, “Akubwera masiku pamene ndidzaphukitsira Davide nthambi yoongoka imene idzakhala mfumu yanzeru ndi yoweruza m'dzikomo mwachilungamo ndi mosakondera. Pa masiku akewo Yuda adzapulumuka, ndipo Israele adzakhala pabwino. Adzamutcha dzina ili lakuti, ‘Chauta ndiye chilungamo chathu.’ ” Chauta akunena kuti, “Akubwera masiku pamene anthu polumbira sazidzatinso, ‘Pali Chauta wamoyo, amene adatulutsa Aisraele ku dziko la Ejipito!’ Koma azidzati, ‘Pali Chauta wamoyo, amene adatulutsa Aisraeli ku dziko lakumpoto, ndi ku maiko konse kumene adaŵabalalitsira.’ Ndithu ndidzaŵabwezera ku malo amene ndidapatsa makolo awo.” Kunena za aneneri, mtima wanga wasweka, m'nkhongono mwachita kuti zii! Ndakhala ngati munthu woledzera, munthu wosokonezeka ndi vinyo, chifukwa cha Chauta ndi mau ake oyera. Dziko lino ladzaza ndi anthu achigololo. Chifukwa cha temberero la Chauta m'dziko mwagwa chilala, mabusa akuchipululu auma. Amene amangothamangira zoipa, amalimbikira kuchita zosalungama. “Zoonadi, aneneri ndiponso ansembe, onsewo saopa Mulungu. Ndaŵapeza akuchita zoipa ngakhale m'Nyumba mwanga,” akutero Chauta. “Nchifukwa chake njira zao zidzakhala zoterera. Adzaŵapirikitsira kumdima kumene akagwe. Ndidzaŵaonetsa ndoza pa nthaŵi ya chilango chao,” akuterotu Chauta. “Pakati pa Aneneri a ku Samariya ndaonapo choipa ichi: ankalosa m'dzina la Baala, motero adasokeza anthu anga Aisraele. Pakati pa aneneri a ku Yerusalemunso ndaonapo chinthu choopsa kwambiri: amachita zigololo, amanena bodza, ndipo amalimbitsa mtima anthu ochita zoipa, kotero kuti palibe amene amaleka machimo ake. Kwa Ine onsewo ali ngati anthu a ku Sodomu ndi Gomora.” Chifukwa cha zimenezi, ponena za aneneri ameneŵa, Chauta akuti, “Ndidzaŵadyetsa dzoŵaŵa ndi kuŵamwetsa madzi azumu, chifukwa zoipa zimene zaŵanda m'dziko lonse zachokera kwa aneneri omweŵa.” Chauta Wamphamvuzonse akuuza anthu kuti, “Musamvere zimene akunena aneneri, iwowo amakuloserani zonyenga. Zimene amakuuzani kuti akuziwona m'masomphenya ndi maganizo ao chabe, si zolankhula Chauta ai. Saleka kuŵauza amene amandinyoza Ine kuti, ‘Zinthu zidzakuyenderani bwino.’ Ndipo amene amaumirira kutsata zofuna za mtima wao amaŵauza kuti, ‘Simudzaona vuto ai.’ ” Ine ndidati, “Mwa aneneriwo ndani amene adakhala nao m'bungwe la Chauta? Ndani adamuwona ndi kumva mau ake? Ndani mwa iwo adasamalako mau ake ndi kuŵamvera? Onani mphepo yamkuntho yochokera kwa Chauta! Onani ukali wake woomba ngati namondwe, udzaomba pa mitu ya anthu oipa. Mkwiyo wa Chauta sudzaleka, mpaka atachita zonse zimene adatsimikiza mumtima mwake. Zimenezi mudzazidziŵa masiku akubweraŵa.” Chauta adati, “Aneneri ameneŵa sindidaŵatume ndine, komabe ankathamanga uku ndi uku ndi mithenga yao. Sindidalankhule nawo, komabe ankalosa. Akadakhala nane pa bungwe langa, bwenzi atalalikadi mau anga kwa anthu anga. Bwenzi ataŵachotsa m'njira zao zoipa, kuti aleke machimo ao.” Chauta akuti, “Kodi ndimakhala Mulungu pokhapokha ndikakhala pafupi, koma ndikakhala patali ndiye kuti sindinenso Mulungu? Kodi munthu nkubisala pobisika potani, pamene Ine sindingathe kumuwona? Kodi Ine sindili ponseponse, kumwamba ndi pa dziko lapansi pano?” Akuterotu Chauta. “Ndamva zimene aneneri akulankhula, aneneri amene akulosa zabodza m'dzina langa, nkumafuula kuti, ‘Ndalota, ndalota.’ Kodi zabodzazi adzazisunga mumtima mwao mpaka liti aneneri onamaŵa, amene amalosa zonyenga za mumtima mwao? Aneneri ameneŵa amakhulupirira kuti anthu anga adzandiiŵala akamamva zamalotozo, monga momwe makolo ao adaiŵalira dzina langa pomapembedza Baala. Ngati mneneri walota maloto, afotokoze maloto akewo. Koma amene ali ndi mau anga, alalike mau angawo moona. Kodi mungu ungafanane ndi tirigu?” Akuterotu Chauta. “Kodi suja mau anga amatentha ngati moto? Kodi suja mau anga ali ngati nyundo imene imaphwanya thanthwe? “Nchifukwa chake ndikuŵakana aneneri amene amaberana mau iwo okhaokha nkumati mauwo ndi a Ineyo. Ndikuŵatsutsa aneneri amene amakonda kulankhula zamabodza, namanena kuti, ‘Ameneŵa ndiwo mau a Chauta.’ Ndikuŵakana aneneri amene amalota zabodza, namasimbira anthu anga ndi kumaŵasokeza ndi mabodza aowo. Sindidaŵatume ndine kapena kuŵalamula, ndipo sathandiza anthu mpang'ono pomwe,” akuterotu Chauta. Chauta adauza Yeremiya kuti, “Anthu ameneŵa, kaya ndi mneneri, kaya ndi wansembe, akakufunsa kuti, ‘Kodi uthenga wolemetsa wa Chauta ukuti chiyani?’ Udzayankhe kuti, ‘Inuyo ndiye katundu wolemetsa Chauta, ndipo adzakutayani,’ akuterotu Chauta. Ndipo mneneri, wansembe, kapena munthu wina aliyense, wonena kuti, ‘Nawu uthenga wolemetsa wa Chauta,’ ameneyo ndidzamulanga pamodzi ndi banja lake. Koma mau amene aliyense azifunsa mnzake kapena mbale wake akhale akuti, ‘Kodi Chauta wanena zotani?’ Koma musanenanso kuti ‘Nawu uthenga wolemetsa wa Chauta.’ Uthenga wa aliyense ndi mau a iye mwini, motero inuyo mudapotoza mau a Mulungu wamoyo, Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wathu. Tsono iwe Yeremiya udzamufunse mneneri kuti, ‘Kodi Chauta wayankha zotani?’ Kapena kuti, ‘Kodi Chauta wanena zotani?’ Koma ngati munena kuti, ‘Nawu uthenga wolemetsa wa Chauta,’ Chautayo akuti, ‘Popeza kuti mwanena mau akuti nawu uthenga wolemetsa wa Chauta, pamene ndidakuuzani kuti musanene mau ameneŵa, pamenepo Ine mwini ndidzakunyamulani ngati katundu wolemetsa nkukutayani kutali. Ndidzakuchotsani pamaso panga inuyo pamodzi ndi mzinda umene ndidakupatsani inu ndi makolo anu. Ndidzakunyozani mpaka muyaya, ndikakuchititsani manyazi osaiŵalika.’ ” Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, adaatenga ukapolo Yehoyakini, mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda, kuchoka naye ku Yerusalemu. Adaatenganso ukapolo akalonga onse a ku Yuda, anthu aluso ndi akatswiri enanso kupita nawo ku Babiloni. Nthaŵi imeneyo Chauta adandiwonetsa zinthu zina m'masomphenya, zinthuzo ndi izi: ndidaona madengu aŵiri a nkhuyu ali pakhomo pa Nyumba ya Chauta. M'dengu lina munali nkhuyu zabwino kwambiri, ngati nkhuyu zoyambirira kupsa. Koma m'dengu linalo munali nkhuyu zoipa kwambiri, zosatinso nkudyeka. Chauta adandifunsa kuti, “Iwe Yeremiya, kodi ukuwona chiyani?” Ine ndidayankha kuti, “Ndikuwona nkhuyu zabwino kwambiri, ndi zinanso zoipa kwambiri, zosatinso nkudyeka.” Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Ine Chauta, Mulungu wa Israele, ndikunena kuti, Akapolo a ku Yuda amene ndidaŵachotsa ku malo ano, kupita nawo ku dziko la Ababiloni, ndikuŵafanizira ndi nkhuyu zabwinozi. Ndidzachita chotheka kuti ndiŵachitire zabwino ndi kuŵabwezeranso ku dziko lao. Ndidzaŵamanga osati kuŵapasula. Ndidzaŵakhazikitsa, osati kuŵazula ai. Ndidzaŵapatsa mtima woti azidziŵa kuti ndine Chauta. Iwowo adzakhala anthu anga, Ine ndidzakhala Mulungu wao, pakuti adzabwera kwa Ine ndi mtima wao wonse. “Koma monga nkhuyu zoipa zija, zosatinso kudyekazi, ndimo m'mene ndidzalangire Zedekiya mfumu ya ku Yuda, pamodzi ndi akalonga, ndi onse otsala a mu Yerusalemu amene ali m'dziko lino, ndiponso Ayuda amene akukhala m'dziko la Ejipito. Ndidzaŵasandutsa chinthu chonyansa kwa anthu a maufumu onse a pa dziko lapansi, chinthu chonyozeka, chinthu chopanda pake, chinthu chomachiseka ndi chotembereredwa kulikonse kumene ndidzaŵapirikitsire. Ndidzaŵapha ndi nkhondo, njala ndi mliri, mpaka onsewo nditaŵapululiratu m'dziko limene ndidaŵapatsa iwowo ndi makolo ao.” Naŵa mau amene adadza kwa Yeremiya, onena za anthu onse a ku Yuda. Mauŵa adafika chaka chachinai cha ufumu wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya ku Yuda, ndiye kuti chaka choyamba cha ufumu wa Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni. Mneneri Yeremiya adauza anthu onse a ku Yuda ndi onse okhala ku Yerusalemu kuti, “Pa zaka 23, kuyambira chaka cha 13 cha ufumu wa Yosiya mwana wa Amoni mfumu ya ku Yuda, mpaka lero lino, ndakhala ndikulandira mau a Chauta ndi kumavutika nkukuuzani, koma inu simudamvere. Inu simudamvere kapena kutchera khutu, ngakhale kuti Chauta sadaleke kukutumirani aneneri, atumiki ake. Aneneriwo ankati, ‘Aliyense mwa inu akaleka makhalidwe ake oipa ndi ntchito zake zoipa, ndiye kuti mudzakhala m'dziko limene Chauta adakupatsani inu ndi makolo anu mpaka muyaya. Musamatsate milungu ina, kumaitumikira ndi kumaipembedza. Musamapute mkwiyo wanga ndi mafano opanga ndi manja anu. Tsono Ine sindidzakuwonongani.’ Komabe simudandimvere. Mudaputa mkwiyo wanga ndi mafano amene mudapanga ndi manja anu, motero mudadziwononga nokha,” akuterotu Chauta. Motero Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Chifukwa choti simudamvere mau anga, ndidzaitana mafuko onse akumpoto, pamodzi ndi mtumiki wanga Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni. Ndidzaŵatuma kuti adzathire nkhondo dzikoli ndi anthu ake, ndiponso anthu a mitundu ina yozungulira dzikoli. Ndidzaŵaononga kwathunthu ndi kuŵasandutsa chinthu chonyansa, chonyozeka ndiponso chochititsa manyazi mpaka muyaya. Ndidzathetsa chimwemwe chonse ndi kusangalala konse pakati pao. Ndidzaletseratu mau achikondwerero a mkwati wamwamuna ndi mkwati wamkazi. Sikudzamvekanso phokoso la mphero, ndipo ndidzazima nyale zonse. Dziko lonseli lidzakhala chipululu ndi bwinja. Pa zaka makumi asanu ndi aŵiri mitundu imeneyi idzatumikira mfumu ya ku Babiloni. Zaka makumi asanu ndi aŵirizo zitatha, ndidzailanga mfumu ya ku Babiloniyo pamodzi ndi anthu ake chifukwa cha zoipa zao, ndipo dziko lao ndidzalisandutsa bwinja mpaka muyaya. Ndidzachita zonse zimene ndidanena zokhudza dziko limenelo, zonse zimene zidalembedwa m'bukumu, ndiponso zonse zimene mneneri Yeremiya adalosa zotsutsa anthu ameneŵa. Iwo adzakhala akapolo a anthu a mitundu yochuluka ndi a mafumu otchuka. Motero ndidzaŵabwezera potsata zochita zao ndi ntchito za manja ao.” Chauta, Mulungu wa Israele, adandiwuza kuti, “Tenga chikho ichi chodzaza ndi mkwiyo wanga, ndipo ukamwetse anthu a mitundu yonse kumene nditi ndikutume. Atamwa, adzayamba kudzandira ndipo adzachita misala chifukwa cha nkhondo imene ndikutumiza pakati pao.” Tsono ndidalandira chikhocho kumanja kwa Chauta ndipo ndidapatsa anthu a mitundu yonse, kuti amwe monga momwe Chauta adaandilamulira. Adandituma ku Yerusalemu, ku mizinda ya ku Yuda, kwa mafumu ake ndi kwa akalonga ake, kuti ndiŵasandutse ngati bwinja, ndi chinthu chonyozeka ndi chomachiseka monga m'mene aliri tsopanomu. Adanditumanso kwa Farao, mfumu ya ku Ejipito, kwa nduna zake, kwa akalonga ake, kwa anthu ake onse, ndi kwa anthu a mitundu ina yachilendo yokhala pakati pao. Adanditumanso kwa mafumu onse a ku dziko la Uzi, kwa mafumu onse a Afilisti, ndiye kuti ku Asikeloni, ku Gaza, ku Ekeroni ndi ku chigawo chotsala cha ku Asidodi. Adanditumanso ku Edomu, ku Mowabu ndiponso kwa Aamoni. Adandituma kwa mafumu onse a ku Tiro ndi Sidoni, ndiponso kwa mafumu a maiko a m'mbali mwa nyanja, ndiye kuti ku Dedani, ku Tema, ku Buzi ndi kwa onse ometa cham'mbali. Adanditumanso kwa mafumu onse a ku Arabiya ndi kwa ena aja okhala m'chipululu. Adandituma kwa mafumu onse a ku Zimiri, kwa mafumu onse a ku Elamu, kwa mafumu onse a ku Mediya, kwa mafumu onse akumpoto, akufupi ndi akutali omwe, ndi kwa maufumu onse a dziko lonse lapansi. Potsiriza, atamwa onsewo, idzamwe ndi mfumu ya ku Babiloni. “Kenaka udzaŵauze kuti, Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, ‘Imwani, muledzere, musanze, mugwe osadzukanso, chifukwa cha nkhondo imene ndikutumiza pakati panu.’ ” “Akakana kulandira chikho kumanja kwako kuti amwe, uŵauze kuti, Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, Muyenera kumwa! Tsopanotu ndiyamba ndalanga mzinda umene umadziŵika ndi dzina langa. Kodi mukuganiza kuti inuyo simudzalangidwa? Iyai, simungathe kupulumuka. Ndithu, nditumiza nkhondo kwa anthu onse okhala pa dziko lapansi,” akutero Chauta Wamphamvuzonse. “Tsono iwe, ulengeze mau oŵatsutsa, uŵauze kuti, ‘Chauta adzakhuluma kumwamba, mau ake adzamveka ngati bingu kuchokera ku malo ake opatulika. Zoonadi, adzakhuluma, kukalipira anthu ake, adzafuula kwambiri ngati anthu oponda mphesa, polimbana ndi anthu onse a pa dziko lapansi. Phokoso lalikululo lidzamveka pa dziko lonse lapansi, chifukwa Chauta akuŵazenga mlandu anthu a mitundu yonse. Akuti aweruza anthu onse, ndipo oipa adzaphedwa ndi lupanga, akuterotu Chauta.’ ” Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Onani, tsoka likuti likachoka pa mtundu wina likukagwa pa mtundu winanso. Ndipo ku malekezero a dziko lapansi kukuyambika mphepo yamkuntho.” Pa tsiku limenelo, onse ophedwa ndi Chauta adzangoti vuu pa dziko lonse lapansi. Palibe amene adzaŵalire, kapena kukaŵaika m'manda. Adzangosiyidwa ngati ndoŵe ponseponse. Inu abusa lirani kwambiri, fuulani kwamphamvu. Inu atsogoleri a anthu anga, dzolani phulusa. Nthaŵi yanu yokaphedwa yafika, ndipo mudzachita kuphedwa ngati nkhosa zamphongo. Abusawo adzasoŵa kothaŵira, eniake a nkhosa adzasoŵa njira yopulumukira. Mverani, abusa akulira, eniake a nkhosa akulira kwambiri, pakuti Chauta akuwononga busa lao. Makola ao a nkhosa, amene adaali pa mtendere, akusanduka mabwinja chifukwa cha ukali woopsa wa Chauta. Chauta waŵasiya anthu ake ngati mkango wosiya phanga lake, ndipo dziko lao lasanduka chipululu, chifukwa cha mazunzo a nkhondo ndi mkwiyo woopsa wa Chauta. Pamene Yehoyakimu, mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda, adayamba kulamulira, Chauta adauza Yeremiya kuti, “Kaime m'bwalo la Nyumba ya Chauta. Ndipo ukalankhule kwa anthu onse okhala m'mizinda ya ku Yuda, amene amakapembedza ku Nyumba imeneyo. Ukaŵauze zonse zimene ndakulamula kuti ukanene, osasiyapo kanthu. Mwina mwake nkutheka kuti adzamvera, ndipo aliyense adzaleka machimo ake. Tsono ndidzaleka osaŵapatsa chilango chimene ndidaati ndiŵalange nacho, chifukwa cha ntchito zao zoipa. Ukaŵauze kuti, Chauta akuti: Ngati simundimvera Ine, ngati simutsata malamulo amene ndidakupatsani, ngati simumvera mau a aneneri, atumiki anga, amene ndakhala ndikuŵatuma kwa inu, ngakhale kuti inu simunkaŵamvera, ndiye kuti Nyumba ino ndidzaiwononga monga m'mene ndidaonongera Silo. Ndipo mzinda uno ndidzausandutsa chinthu chonyozeka kwa mitundu yonse ya pa dziko lapansi!” Tsono ansembe, aneneri, pamodzi ndi anthu ena ambiri, adamva Yeremiya akulankhula mau ameneŵa m'Nyumba ya Chauta. Yeremiya atatsiriza kulankhula zimene Chauta adamlamula kuti auze anthu onse, ansembe, aneneri ndi anthu onsewo adamgwira, namuuza kuti, “Ukuyenera kuphedwa. Chifukwa chiyani walosa m'dzina la Chauta kuti Nyumba ino idzaonongedwa ngati Silo, ndipo kuti mzinda uno udzasanduka wopanda anthu, ngati chipululu?” Motero anthu onse adasonkhana nazinga Yeremiya m'Nyumba ya Chauta. Akuluakulu a ku Yuda atamva zimene zinkachitikazo, adanyamuka kuchokera ku nyumba ya mfumu kupita ku Nyumba ya Chauta, nakakhala pa bwalo lao ku chipata chatsopano cha Nyumba ya Chauta. Pamenepo ansembe ndi aneneri adauza akuluakuluwo ndi anthu ena onse kuti, “Munthu ameneyu ndi woyenera kumupha, chifukwa choti amalosa zoipa za mzinda uno, monga inu nomwe mwadzimvera.” Tsono Yeremiya adauza akuluakulu aja ndi anthu onse kuti, “Chauta adachita kundituma kuti ndilengeze mau onse mwamvaŵa oinena Nyumba ya Mulungu ino pamodzi ndi mzindawu. Ngati tsopano mukonza makhalidwe anu ndi ntchito zanu zomwe, ndi kuyamba kumvera mau a Chauta Mulungu wanu, ndiye kuti Iye adzakhululuka osakulangani monga m'mene adaaganizira. Ineyo ndili m'manja mwanu. Mundichite chilichonse chimene chikukomereni. Koma tsono mudziŵe kuti mukangondipha, ndiye kuti inuyo pamodzi ndi mzinda uno ndi anthu onse okhalamo, mudzapalamula mlandu wokhetsa magazi a munthu wosalakwa. Ndithudi, nzoona kuti Chauta ndiye adandituma kwa inu, kuti mumve zonse ndikunenazi.” Pamenepo akuluakuluwo ndi anthu ena adauza ansembe ndi aneneri kuti, “Munthuyu sayenera kufa, popeza kuti walankhula nafe m'dzina la Chauta, Mulungu wathu.” Akuluakulu ena am'dzikomo adaimiriranso nauza anthu onse amene adasonkhanawo kuti, “Nthaŵi imene Hezekiya anali mfumu ya ku Yuda, Mika wa ku Moreseti ankalosa, ndipo adauza anthu onse a ku Yuda kuti Chauta Wamphamvuzonse akuti, “ ‘Ziyoni adzalimidwa ngati munda. Yerusalemu adzasanduka bwinja, phiri la Nyumba ya Mulungu lidzasanduka nkhalango.’ Nanga kodi mfumu Hezekiya ndi anthu onse a ku Yuda adamupha amene uja? Kodi suja mfumu idaopa Chauta nipempha kuti aikomere mtima? Ndipo suja Chauta adaleka osaŵapatsa chilango chimene adaati aŵalange nacho? Koma ife tili pafupi kudziitanira tsoka lalikulu.” Padaalinso munthu wina amene ankalosa m'dzina la Chauta, dzina lake Uriya mwana wa Semaya wa ku Kiriyati-Yearimu. Iyeyo adaalosanso zodzagwera mzinda uno ndi dziko lino monga momwe adachitira Yeremiya. Mfumu Yehoyakimu ndi akuluakulu ake onse ndiponso ankhondo ake, atamva zimene adaanena, adaafuna kumupha. Uriya atamva choncho, adachita mantha, nathaŵira ku Ejipito. Komabe mfumu Yehoyakimu adatuma Elinatani mwana wa Akibori, pamodzi ndi anthu ena, ku Ejipito. Iwowo adakagwira Uriya ku Ejipito komweko, nkubwera naye kwa mfumu Yehoyakimu. Mfumuyo idalamula kuti Uriyayo aphedwe, ndipo mtembo wake adakauika ku manda a anthu wamba. Koma Ahikamu mwana wa Safani ndiye adatchinjiriza Yeremiya, motero sadaperekedwe kwa anthu kuti amuphe. Pamene Zedekiya, mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda adayamba kulamulira, Chauta adalankhula ndi Yeremiya namuuza kuti, “Tenga nsinga zachikopa ndi mitengo ya goli, uzimange m'khosi mwako. Tsono utumize uthenga kwa mafumu a ku Edomu, Mowabu, Amoni, Tiro ndi Sidoni, kudzera mwa amithenga amene abwera ku Yerusalemu kwa Zedekiya, mfumu ya ku Yuda. Uŵauze kuti akadziŵitse atsogoleri ao kuti Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akuuza atsogoleriwo kuti: Ndidalenga dziko lapansi ndi mphamvu zanga ndi nyonga zanga. Ndidalenga anthu ndi nyama pa dziko lapansi, ndipo ndimalipereka kwa amene ndimamuwona kuti ndi woyenera. Tsopano ndapereka maiko onseŵa kwa Nebukadinezara mtumiki wanga, mfumu ya ku Babiloni. Ndampatsanso nyama zonse zakuthengo kuti zizimtumikira. Anthu a mitundu yonse adzamtumikira iyeyo, mwana wake ndi mdzukulu wake, mpaka itakwana nthaŵi yoti dziko lake liwonongedwe. Pamenepo anthu a mitundu yambiri ndi mafumu amphamvu adzagonjetsa ufumu wakewo. “Koma ngati anthu a mtundu wina uliwonse kapena a dziko lina lililonse adzakana kutumikira Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, kapena kugonjera ulamuliro wake, Ineyo ndidzaŵalanga ndi nkhondo, njala ndi mliri, mpaka nditaŵapereka m'manja mwake kotheratu,” akuterotu Chauta. “Nchifukwa chake musaŵamvere aneneri anu, oombeza anu, otanthauza maloto, amaula ndi amatsenga anu, akamakuuzani kuti musadzatumikire mfumu ya ku Babiloni. Ndithudi, amakuloserani zabodza, kotero kuti adani adzakuchotsani m'dziko lanu, kupita nanu kutali. Ndidzakupirikitsani ndipo mudzaonongeka. Koma mtundu wina uliwonse umene udzagonjera mfumu ya ku Babiloni ndi kumaitumikira, ndidzausiya kuti ukhale m'dziko lake, kuti uzilima ndi kumakhala kumeneko,” akuterotu Chauta. “Mau okhaokhawo ndidauzanso Zedekiya mfumu ya ku Yuda, ndidati: Mugonjere ulamuliro wa mfumu ya ku Babiloni ndi kumaitumikira iyoyo pamodzi ndi anthu ake. Mukatero mudzapulumutsa moyo wanu. Nanga iweyo ndi anthu ako, muferenji ndi nkhondo, njala ndi mliri, zimene Chauta waopsera mtundu wina uliwonse wosatumikira mfumu ya ku Babiloni? Musaŵamvere aneneri okuuzani kuti musadzatumikire mfumu ya ku Babiloni. Akukuloserani zabodza. Sindidaŵatume ndine, ngakhale iwowo akuti amalosa m'dzina langa. Motero ndidzakupirikitsani, ndipo mudzaonongeka inuyo pamodzi ndi aneneri amene amakuloseraniwo. “Pambuyo pake ndidauza ansembe pamodzi ndi anthu ena onse kuti Chauta akunena kuti: Musaŵamvere aneneri anu amene amakuuzani kuti, ‘Ziŵiya za ku Nyumba ya Chauta adzazibwezanso mwamsanga kuchokera ku Babiloni.’ Iwowo akungokuloserani zabodza. Musaŵamvere, muzitumikira mfumu ya ku Babiloni ndipo mupulumutse moyo wanu. Chifukwa chiyani mzindawu usanduke bwinja? Ngati iwo ndi aneneridi ndipo ngati ali ndi mau a Chauta, apemphere kwa Chauta Wamphamvuzonse kuti ziŵiya zimene zidatsala m'Nyumba ya Chauta ndiponso m'nyumba ya mfumu ku Yerusalemu zisatengedwe kupita ku Babiloni. Chauta Wamphamvuzonse ndiye akunena za mizati, chimbiya, maphaka ndi ziŵiya zonse zimene zidatsala mumzindamu. Zimenezi Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni sadazitenge pa nthaŵi imene ankatenga ukapolo Yehoyakini mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda, kuchoka naye ku Yerusalemu kupita naye ku Babiloni pamodzi ndi atsogoleri a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu. Zoonadi, ameneŵa ndiwo mau a Chauta Wamphamvuzonse onena za ziŵiya zimene zidatsala m'Nyumba ya Chauta, m'nyumba ya mfumu ya ku Yuda ndiponso mu Yerusalemu, akuti, ‘Zidzatengedwa kupita ku Babiloni. Ndipo zidzakhala kumeneko mpaka tsiku limene ndidzazikumbukenso. Apo ndidzazitenganso ndi kudzazibwezanso ku malo ano,’ ” akuterotu Chauta. Chaka chomwecho mwezi wachisanu wa chaka chachinai, Zedekiya ataloŵa ufumu wa ku Yuda, Hananiya mwana wa Azuri mneneri wa ku Gibiyoni, adalankhula nane ku Nyumba ya Chauta. Ansembe ndi anthu onse alikumva, iye adati, Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, “Ndathyola goli laukapolo la mfumu ya ku Babiloni. Zisanathe zaka ziŵiri, ndidzabwezera ziŵiya zonse za ku Nyumba yanga ku malo ano, zimene Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, adazichotsa kuno kupita nazo ku Babiloni. Ndidzambwezanso ku malo ano Yehoyakini, mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda. Ndidzabweza akapolo onse ochokera ku Yuda amene adatengedwa kupita ku Babiloni. Motero ndidzathyola goli laukapolo la mfumu ya ku Babiloni.” Apo mneneri Yeremiya adayankha mneneri Hananiya pamaso pa ansembe ndi anthu onse amene anali m'Nyumba ya Chauta. Adati, “Inde momwemo! Chauta achitedi choncho. Chauta achitedi zimene walosazi, pakubwezera ziŵiya za ku Nyumba yake ndi akapolo onse ku malo ano kuchokera ku Babiloni. Komabe ungomva zimene nditi ndikuuze iweyo ndi anthu onse. Aneneri amene adatsogola kale ankalosa za nkhondo, za njala ndi za mliri, zodzagwera maiko ambiri ndi maufumu otchuka. Koma ngati mneneri alosa za mtendere, zimene walosazo zikachitikadi, pamenepo zidzadziŵika kuti Chauta adamtumadi.” Pamenepo mneneri Hananiya adachotsa goli m'khosi mwa mneneri Yeremiya nalithyola. Adauza anthu onse kuti, “Chauta akuti, ‘Umu ndimo m'mene ndidzathyolera goli laukapolo la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni. Ndidzalichotsa m'khosi mwa anthu a mitundu yonse zisanathe zaka ziŵiri.’ ” Zitatero mneneri Yeremiya adachokapo. Patapita nthaŵi pang'ono Hananiya atathyola goli m'khosi mwa Yeremiya, Chauta adauza Yeremiya kuti, “Pita ukamuuze Hananiya mau a Chauta akuti, ‘Iweyo wathyola goli lamtengo, m'malo mwake Ine ndidzaika goli lachitsulo. Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, Ndaika goli lachitsulo m'khosi mwa anthu a mitundu yonseyi, kuti azitumikira Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni. Adzamutumikiradi, ndipo ndampatsanso ulamuliro ngakhale pa nyama zakuthengo.’ ” Tsono Yeremiya adauza Hananiya kuti, “Mvera, iwe Hananiya, Chautatu sadakutume, ndipo iweyo wanyenga anthuŵa kuti azimvera ulosi wabodza. Nchifukwa chake Chauta akunena kuti, ‘Chenjera, ndidzakuchotsa pa dziko lapansi. Ufa chaka chino chisanathe, chifukwa chakuti wakhala ukulalikira zopandukira Chauta.’ ” Zidachitikadi kuti mneneri Hananiya adafa chaka chomwecho, mwezi wachisanu ndi chiŵiri. Yeremiya adatumiza kalata kuchokera ku Yerusalemu yopita kwa atsogoleri amene anali ku ukapolo, ndiponso kwa ansembe, aneneri, ndi anthu ena onse amene Nebukadinezara adaaŵatenga ukapolo ku Yerusalemu kupita nawo ku Babiloni. Zimenezi zidachitika pamene Yehoyakini ndi mfumukazi, nduna za mfumu ndi akuluakulu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu, ndiponso anthu aluso ndi osula, anali atachoka ku Yerusalemu. Yeremiya kalatayo adapatsira Elasa mwana wa Safani, ndi Gemariya mwana wa Hilikiya, amene Zedekiya mfumu ya ku Yuda adaaŵatuma ku Babiloni kwa mfumu Nebukadinezara. M'kalatamo adaalembamo kuti, “Anthu onse a ku Yerusalemu, amene adatengedwa ukapolo kupita ku Babiloni, Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akuŵauza kuti, ‘Mangani nyumba, muzikhalamo. Limani minda, mudye zipatso zake. Mukwatire, ndipo mubale ana aamuna ndi ana aakazi. Ana aamunawo muŵasankhire akazi, ana aakaziwo muŵasankhire amuna, kuti abale ana aamuna ndi ana aakazi. Ndipo muchulukane kumeneko, osachepa. Muzikometsa ku mizinda kumene ndidakupirikitsirani ku ukapoloko, kuti zonse zizikuyenderani bwino. Muzipempherera mizindayo kwa Chauta, chifukwa choti mizindayo ikakhala pa mtendere, inunso mudzakhala pabwino. Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, Aneneri asakunyengeni, ngakhale oombeza amene ali pakati panu, ndipo musamvere maloto ao. Ndithu amakuloserani zabodza m'dzina langa, Ine sindidaŵatume,’ ” akutero Chauta. Chauta akunena kuti, “Zitatha zaka makumi asanu ndi aŵiri ku Babiloni, ndidzakuyenderani ndi kuchitadi zimene ndidakulonjezani zija, ndipo ndidzakubwezerani ku malo ano. Zoona, Ine ndiye amene ndimadziŵa zimene ndidakukonzerani, zakuti mudzakhala pabwino osati poipa, kuti mukhale ndi chiyembekezo chenicheni pa zakutsogolo. Nthaŵi imeneyo mudzandiitana ndi kumanditama mopemba, ndipo ine ndidzakumverani. Mudzandifunafuna, ndipo mudzandipeza. Mukadzandifunafuna ndi mtima wanu wonse, mudzandipezadi,” akuterotu Chauta. “Ndidzakubwezerani zabwino zanu, ndi kukusonkhanitsani kuchokera ku mitundu ina ya anthu ndi kumalo konse kumene ndidakupirikitsirani. Ndidzakubwezerani kumalo kumene mudaali, ndisanakutumizeni ku ukapolo.” Inu mumanena kuti, “Chauta adatipatsa aneneri athu ku Babiloni.” Koma Chauta alipo ndi mau pa za mfumu imene ikukhala pa mpando waufumu wa Davide, ndi pa za anthu onse okhala mu mzinda uno, ndiye kuti anzanu a m'dzikomo amene sadatengedwe nao ukapolo. Akunena kuti, “Ndidzaŵapha ndi nkhondo, njala ndi mliri. Ndidzaŵasandutsa ngati nkhuyu zoola kwambiri, zosatinso nkudyeka ai. Ndidzaŵapha ndi nkhondo, njala ndi mliri, ndipo ndidzaŵasandutsa chinthu chonyansa kwa anthu a maufumu onse a pa dziko lapansi. Adzakhala otembereredwa ndi ochititsa mantha, oŵaseka ndi onyozeka, pakati pa mitundu yonse ya anthu kumene ndidaŵapirikitsira. Izi zidzatero chifukwa sadamvere mau anga, pamene Ine ndidakhala ndikuŵatumizira aneneri, atumiki anga. Koma inunso simudamvere,” akuterotu Chauta. “Nchifukwa chake tsono inu akapolo nonse amene ndidakutengani ukapolo kuchoka ku Yerusalemu kupita ku Babiloni, mverani mau a Ine Chauta. “Chauta Wamphamvuzonse wanenapo mau pa za Ahabu mwana wa Kalaya, ndi za Zedekiya mwana wa Maseiya, amene ankakuloserani zabodza m'dzina la Chautayo. Akuti, Ndidzaŵapereka kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndipo iyeyo adzaŵapha inu mukupenya. Chifukwa cha anthu aŵiriwo, maina ao azidzaŵatchula anthu a ku Yuda okhala ku Babiloni potemberera anzao. Azidzati, ‘Chauta achite nawe monga m'mene adachitira ndi Zedekiya ndi Ahabu amene mfumu ya ku Babiloni adaŵatentha!’ Zoonadi makhalidwe ao ku Israele analidi oipa, ankachita chigololo ndi akazi a eniake, ankalosa zabodza m'dzina langa, Ine osaŵalamula. Ine ndikuzidziŵa, ndingathe kuzichitira umboni zimenezi,” akuterotu Chauta. Semaya wa ku Nehelamu ukamuuze kuti, “Mau a Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, ndi aŵa akuti: Iweyo udatumiza kalata m'dzina lako kwa anthu onse a ku Yerusalemu, kwa Zefaniya wansembe mwana wa Maseiya, ndi kwa ansembe onse. M'kalatamo udanena kuti Chauta wakuika iwe Zefaniya, kuti ukhale wansembe m'malo mwa wansembe Yehoyada. Wakuika kuti ukhale kapitao woyang'anira Nyumba ya Chauta. Uzimponya m'ndende ndi kumuveka goli munthu aliyense wamsala amene amadziyesa mneneri. Nanga chifukwa chiyani tsono sudamchite zimenezi Yeremiya wa ku Anatoti, amene amakhala ngati mneneri pakati panu? Ifetu ku Babiloni kuno Yeremiyayo watitumizira mau akuti: Ukapolo wanu ukhala wautali. Mangani nyumba zoti muzikhalamo, ndipo limani minda kuti muzidya zipatso zake.” Kalata ya Semayayo wansembe Zefaniya adaiŵerengera pamaso pa mneneri Yeremiya. Tsono Chauta adauza Yeremiya kuti, “Utume uthenga kwa akapolo onse, uŵauze mau a Chauta onena za Semaya wa ku Nehelamu, akuti, Semaya wakuloserani, ngakhale sindidamtume, ndipo wakunyengani kuti muzikhulupirira zabodza. Nchifukwa chake Ine Chauta ndikunena kuti: Ndidzamlanga Semaya pamodzi ndi zidzukulu zake. M'banja lakelo palibe munthu amene adzakhale pakati pa mtundu uno wa anthu, amene adzaone zabwino zomwe ndidzachitira anthu anga, chifukwa iyeyo walalika zondipandukira,” akuterotu Chauta. Chauta adauza Yeremiya kuti, “Ine Chauta, Mulungu wa Israele, ndikunena kuti, Lemba m'buku zonse zimene ndakuuza. Nthaŵi ikubwera yoti ndidzaŵabwezere anthu anga, Israele ndi Yuda, ku dziko limene ndidapatsa makolo ao, ndipo lidzakhaladi lao.” Mau amene akunena za Israele ndi Yuda ndi aŵa: “Tamva kulira kwankhaŵa, kufuula kwamantha, ndipo palibe mtendere paliponse. Funsani kuti muzindikire, Kodi munthu wamwamuna angathe kubala mwana? Nanga nchifukwa chiyani ndikuwona munthu wamwamuna aliyense atagwira manja pa mimba ngati mkazi pa nthaŵi yake yochira? Chifukwa chiyani nkhope zonse zagwa? Kalanga ine! Tsiku limenelo nlalikulu kwambiri, sipadzakhala lina lofanana nalo. Idzakhala nthaŵi yamavuto kwa Yakobe, komabe adzapulumuka ku mavutowo.” Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Tsiku limenelo ndidzathyola goli laukapolo m'khosi mwao, ndidzadula zingwe zoŵamanga. Aisraele sadzakhalanso akapolo a alendo. Azidzangotumikira Chauta, Mulungu wao, ndi Davide, mfumu yao, amene ndidzaŵasankhulira. “Nchifukwa chake musachite mantha inu a m'banja la Yakobe, mtumiki wanga, musataye mtima inu Aisraele,” akuterotu Chauta. “Ndithu ndidzakupulumutsani kuchokera ku dziko lakutali. Ndidzapulumutsanso zidzukulu zanu kuchokera kudziko kumene ali mu ukapolo. Nonsenu mudzabwereranso, ndipo mudzakhala ndi mtendere popanda okuwopsani. Ine ndili nanu, ndipo ndidzakupulumutsani,” akuterotu Chauta. “Ndidzaononga mitundu yonse ya anthu kumene ndidakubalalitsani, koma inu sindidzakuwonongani kotheratu. Ndidzakulangani potsata chilungamo, sindingakulekerereni osakulangani konse.” Chauta akunena kuti, “Chilonda chanu nchosachizika, bala lanu nlonyeka. Palibe amene angathe kukutetezani pa mlandu wanu. Palibe mankhwala opoletsa chilonda chanu. Palibe mankhwala ochiza nthenda yanu. Abwenzi anu onse akuiŵalani, sakulabadiraninso. Ndakulangani mwankhanza, poti mlandu wanu ndi waukulu, machimo anu ndi ambiri. Chifukwa chiyani mukudandaula nacho chilonda chanu? Bala lanu silingapole ai. Mlandu wanu ndi waukulu, machimo anu ngambiri, nchifukwa chake ndakuchitani zimenezi. Tsono onse amene adakuwonongani inu, ndidzaŵaononga iwonso. Onse okuzunzani adzatengedwa ukapolo. Onse ofunkha zinthu zanu, nawonso zao zidzafunkhidwa. Ndipo onse okusakazani, ndidzachita zoti nawonso aŵasakaze. Koma inuyo, ndidzachiza matenda anu, ndidzapoletsa mabala anu, chifukwa anthu ena amati ndinu otayika, amati, ‘Ndi anthu a ku Ziyoni aŵa, opanda oŵasamala,’ ” akuterotu Chauta. Chauta akunena kuti, “Ndidzabwezeranso a banja la Yakobe ku dziko lao. Ndidzaonetsanso chikondi changa ku malo ake onse. Mzinda wa Yerusalemu uja udzamangidwanso pabwinja pake pompaja. Nyumba yaufumu idzamangidwanso pamalo pake. Anthuwo adzaimba nyimbo zoyamika Chauta, ndipo padzamveka phokoso la chisangalalo. Ndidzaŵachulukitsa, sadzakhalanso oŵerengeka ai. Ndidzaŵapatsa ulemerero, ena sadzaŵanyozanso. Ana ao adzakhalanso monga m'mene adaaliri kale. Mpingo wao wonse ndidzaukhazikitsanso Mwiniwakene. Ndidzalanga onse oŵazunza. Wodzaŵalamulira adzakhala mmodzi mwa iwo. Mtsogoleri wao adzachokera pakati pao. Ineyo ndidzamkokera pafupi nane, ndipo iye adzayandikana nane. Ndanitu angalimbe mtima payekha kuti ayandikane ndi Ine?” Akutero Chauta. “Motero inu mudzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu. “Onani, mphepo yamkuntho ya Chauta! Mkuntho wamphamvu wa kamvulumvulu, ukuwomba pa mitu ya anthu olakwa. Mkwiyo wa Chauta sudzachoka mpaka utatsiriza kuchita zonse zimene mtima wa Chautayo ukufuna. Mudzamvetsa zimenezi masiku akubwerawo.” Chauta akunena kuti, “Pa nthaŵi imeneyo ndidzakhala Mulungu wa mabanja onse a Israele, ndipo iwo adzakhala anthu anga.” Mau a Chauta ndi aŵa, “Anthu amene adapulumuka ku nkhondo, ndidaŵakomera mtima m'chipululu. Pamene Aisraele ankafuna kupumula, Ine ndidaŵaonekera ndili chakutali. Inu Aisraele ndakukondani kwambiri ndi chikondi chopanda malire, ndakhala wokhulupirika kwa inu mpaka tsopano. Ndidzakusamaliraninso inu anthu a ku Israele, motero mudzapezanso bwino. Mudzakondwanso poimba ting'oma tolira, ndipo mudzapita nawo limodzi anthu ovina mwachimwemwe. Mudzalimanso minda yamphesa pa mapiri a Samariya. Alimi adzabzala mphesa ndipo adzadya zipatso zake. Lidzafika tsiku pamene alonda a pa mapiri a Efuremu adzafuula kuti, ‘Tiyeni, tipite ku Ziyoni kwa Chauta, Mulungu wathu!’ ” Chauta akuti, “Imbani mokweza ndi mosangalala chifukwa cha Yakobe. Fuulani chifukwa cha mtundu wopambana mitundu yonse. Lalikani, tamandani ndi kulengeza kuti, ‘Chauta wapulumutsa anthu ake, wasunga otsala a Israele.’ Ndidzaŵatulutsa kuchokera ku dziko lakumpoto. Ndidzaŵasonkhanitsa kuchokera ku malekezero a dziko lapansi. Ndidzasonkhanitsa akhungu ndi opunduka, akazi amene ali ndi pakati ndi amene ali pa nthaŵi yao yochira. Chidzakhala chinamtindi cha anthu obwerera kuno. Adzabwerera kwao akulira, koma Ine ndidzaŵaperekeza ndi mtima wachifundo. Ndidzaŵatsogolera ku mitsinje yodzaza ndi madzi. Sadzaphunthwa, njira yao idzakhala yosalala kwambiri. Ine ndine bambo wake wa Israele, Efuremu ndi mwana wanga wachisamba. “Mverani mau a Chauta, inu anthu a mitundu yonse. Mulalike mauwo ku maiko akutali a m'mbali mwa nyanja. Mulungu amene adabalalitsa Aisraele adzaŵasonkhanitsanso. Adzaŵasamala monga momwe mbusa amasamalira nkhosa zake. Ndithu, Chauta waombola fuko la Yakobe. Adaŵapulumutsa m'mavuto amene sakadatha kutulukamo. Anthuwo adzabwera akuimba mofuula pa mapiri a Ziyoni, adzakhala osangalala kwambiri chifukwa cha zabwino zochuluka zochokera kwa Chauta. Zabwinozo ndi izi: tirigu, vinyo watsopano, mafuta, anaankhosa ndi anaang'ombe. Moyo wao udzakhala ngati munda wothirira, ndipo sadzamvanso chisoni. Anamwali adzavina mokondwa, achinyamata ndi okalamba omwe adzasangalala. Kulira kwao kuja ndidzakusandutsa chimwemwe. Ndidzaŵasangalatsa, ndidzaŵakondwetsa, nkuchotsa chisoni chao. Ansembe ndidzaŵadyetsa chakudya chabwino, ndipo anthu anga adzakhuta zabwino za chifundo changa,” akuterotu Chauta. Mau a Chauta ndi aŵa: “Imvani, kulira kukumveka ku Rama, kulira komvetsa chisoni. Rakele akulira ana ake. Sakutonthozeka, chifukwa choti ana ake asoŵa.” Chauta akunena kuti, “Tonthola, usadzenso misozi. Ndithu udzalandira mphotho ya ntchito zako, akutero Chauta. Ndipo anthu adzabwerako ku dziko la adani. Tsono chikhulupiriro chilipo pa zakutsogolo, zidzukulu zanu zidzabweranso kudziko kuno,” akutero Chauta. “Ndamva Aefuremu akulira mwachisoni kuti, ‘Inu mwatilanga ngati mwanawang'ombe wosaphunzitsidwa, ndipo taphunziradi kumvera. Mutibweze kuti tithe kubwerera, Pakuti inu ndinu Chauta, Mulungu wathu. Tsopano poti tatembenuka mtima, tikumva chisoni. Tsopano poti taphunzira, tikudzigunda pa mtima. Tachita manyazi ndipo tanyazitsidwa, chifukwa cha machimo athu apaubwana.’ Kodi suja Efuremu ndi mwana wanga wapamtima, mwana amene ndimakondwera naye kwambiri? Nthaŵi zonse ndikamamdzudzula, ndimamkumbukirabe ndi chikondi, mwakuti mtima wanga umamlakalaka. Ndimamumvera chifundo chozama zedi,” akuterotu Chauta. “Mudziikire zizindikiro, mudziikire zikwangwani. Muuyang'anitsitse mseuwo, mseu umene mudaadzera popita. Bwerera namwaliwe Israele, bwerera ku mizinda yako ija. Kodi udzakhala ukutepeka mpaka liti, iwe mwana wanga wosakhulupirika? Zoona, Chauta walenga chinthu chatsopano pa dziko lapansi: mkazi ndiye atsogola kufunafuna mwamuna.” Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, “Pamene ndidzabwezeranso anthu ufulu, kudzamvekanso mau ku dziko la Yuda ndi ku mizinda yake. Mau ake adzakhala akuti, ‘Chauta akudalitse iwe malo achilungamo, ndiponso iwe phiri loyera.’ Anthu adzakhala ku Yuda ndi ku mizinda yake, pamodzi ndi alimi ndi oŵeta nkhosa. Ndidzatsitsimutsa anthu ofooka, ndipo anthu anjala ndidzaŵadyetsa chakudya nadzakhuta.” Pamenepo ndidadzuka nkudzati maso mwalamwala, ndipo ndidaona kuti ai ndidaatipha tulo. Chauta akunena kuti, “Ikubwera nthaŵi pamene ndidzachulukitsa anthu ndi ziŵeto mu Israele ndi Yuda. Monga momwe ndidaŵasamalira, kuŵazula, kuŵapasula, kuŵagumula, kuŵaononga ndi kuŵachita zoipa, momwemonso ndidzasamala kuti ndiŵamange ndi kuŵabzalanso,” akuterotu Chauta. “Masiku amenewo anthu sadzanenanso kuti, ‘Makolo adya mphesa zosapsa, koma ana ndiye achita dziru.’ Koma munthu aliyense adzafa chifukwa cha machimo ake. Aliyense wodya mphesa zosapsa, ndi iye yemweyo amene adzachite dziru.” Chauta akunena kuti, “Akubwera masiku pamene ndidzachite chipangano chatsopano ndi anthu a ku Israele ndi a ku Yuda. Sichidzakhalanso ngati chipangano chija chimene ndidaachita ndi makolo ao, pamene ndidaŵagwira padzanja nkuŵatulutsa ku dziko la Ejipito. Chipangano chimenecho iwo adaphwanya, ngakhale ndinali Mbuye wao. Koma chipangano chimene ndidzachite ndi anthu a ku Israele atatha masiku amenewo, ndi ichi: Ndidzaika malamulo anga mwa iwo, ndidzachita kuŵalemba m'mitima mwao. Tsono Ineyo ndidzakhala Mulungu wao, ndipo iwowo adzakhala anthu anga. Nthaŵi imeneyo wina sazidzachitanso kuphunzitsa mnzake kapena mbale wake kuti adziŵe Chauta. Pakuti onsewo, ana ndi akulu omwe adzandidziŵa, Ndidzaŵakhululukira machimo ao, sindidzakumbukiranso machimo aowo,” akuterotu Chauta. Chauta akunenanso kuti, “Iye amene amaŵalitsa dzuŵa masana, amene amaŵalitsa mwezi ndi nyenyezi usiku, amene amavundula nyanja kuti mafunde ake achite mkokomo, ndiye amene dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse. Ngati zochitika zimenezi zilekeka, Ine ndili pomwepo, pamenepo ndiye fuko la Israele lidzathe, ndipo silidzakhalanso mtundu wa anthu pamaso panga mpaka muyaya. Atangopezeka munthu wotha kupima zakumwamba nkufufuza maziko a dziko lapansi, pamenepo Inenso ndidzalitaya fuko lonse la Israele, chifukwa cha zoipa zimene iwo adachita,” akuterotu Chauta. Chauta akuti, “Ikubwera nthaŵi pamene mzinda uja wa Chauta udzamangidwanso kuyambira ku Nsanja ya Hananele mpaka ku Chipata cha Ngodya. Kuyambira pamenepo malire ake adzapitirira mpaka ku phiri la Garebe, nkudzakhota kuloza ku Gowa. Chigwa chonse m'mene amatayiramo mitembo ndi phulusa, ndiponso minda yonse kuyambira ku mtsinje wa Kidroni mpaka ku ngodya ya Chipata cha Kavalo chakuvuma, zonsezo zidzakhala zopatulikira Chauta. Mpakampaka mzinda wa Yerusalemu sudzaonongedwanso kapena kugwetsedwa.” Chauta adalankhula ndi Yeremiya pa chaka cha khumi cha ufumu wa Zedekiya ku Yuda, chimene chinali chaka cha 18 cha ufumu wa Nebukadinezara. Pa nthaŵi imeneyo ankhondo a mfumu ya ku Babiloni ankazinga Yerusalemu ndi zithando zankhondo. Mneneri Yeremiya anali atamtsekera m'bwalo la alonda, m'kati mwa nyumba yaufumu ya ku Yuda. Zedekiya mfumu ya ku Yuda ndiye amene adaamtsekera m'menemo. Mfumuyo idaamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani iwe ukulosa zakuti, Chauta akunena kuti, ‘Mzindawu ndidzaupereka kwa mfumu ya ku Babiloni, ndipo adzaulanda. Zedekiya mfumu ya ku Yuda sadzapulumuka kwa Ababiloni, koma adzaperekedwa ndithu kwa mfumu ya ku Babiloni. Adzaonana naye maso ndi maso nadzalankhula naye. Zedekiya adzatengedwa kupita ku Babiloni, ndipo adzakhala kumeneko mpaka nditamkhaulitsa, akutero Chauta. Ngakhale iye adzamenyane nawo chotani Ababiloniwo, sadzatha kuŵapambana.’ ” Yeremiya adanena kuti, “Chauta adandiwuza kuti Hanamele, mwana wa Asalumu, amalume anga, akudzandiwona, ndipo adzandiwuza kuti, ‘Gula munda wanga wa ku Anatoti, poti iweyo ndiye woyenera kuuwombola.’ Monga momwe Chauta adanenera, Hanamele msuweni wanga adadzandiwonadi ku bwalo la alonda. Iyeyo adati, ‘Gula munda wanga ku Anatoti m'dziko la Benjamini, poti iwe ndiye woyenera kuuwombola kuti ukhale choloŵa chako.’ Tsono ndidadziŵa kuti umenewu unali uthenga wa Chauta uja. Motero ndidagula mundawo ku Anatoti kwa Hanamele msuweni wanga, ndipo mtengo wake unali masekeli asiliva 17. Ndidasaina chipanganocho ndi kuchimata pamaso pa mboni, kenaka nkuyesa ndalamazo pa sikelo. Pambuyo pake ndidatenga makalata anga a chipangano, ina yomata, m'mene munali mau onse a chipangano, ndi ina yosamata. Makalatawo ndidaŵapereka kwa Baruki mwana wa Neriya, mdzukulu wa Maseiya, pamaso pa Hanamele msuweni wanga, pamaso pa mboni zimene zidaasaina chipanganocho, ndiponso pamaso pa Ayuda onse okhala m'bwalo la alonda. Ndidamlangiza Baruki pamaso pa onsewo kuti, Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, walamula kuti iweyo utenge makalata a umboni wa chipanganoŵa, inai yomata inai yosamata, uŵasunge m'mbiya kuti akhale nthaŵi yaitali. Ndithudi Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akutitu idzafika nthaŵi pamene anthu azidzagulanso nyumba, minda ndi mitengo ya mphesa m'dziko lino.” Nditampatsa Baruki, mwana wa Neriya, makalata a chipangano aja, ndidayamba kupemphera kwa Chauta, ndidati, “Ha! Inu Chauta! Mudalenga ndinu dziko lakumwamba ndi dziko lapansi. Mudazilenga ndi dzanja lanu lamphamvu kwambiri. Palibe chokukanikani. Mumaonetsa chikondi chanu chosasinthika kwa anthu osaŵerengeka. Ndipo mumalanga ana chifukwa cha machimo a makolo ao. Inu Mulungu wamkulu ndi wamphamvu, dzina lanu ndinu Chauta Wamphamvuzonse. Zolinga zanu nzazikulu, ndipo ntchito zanu nzamphamvu. Maso anu amaona makhalidwe onse a anthu. Ndipo aliyense mumampatsa mphotho malinga ndi makhalidwe ake ndi ntchito zake. Inu mudachita zizindikiro zozizwitsa ndi ntchito zododometsa ku Ejipito, ndipo mwakhala mukuzichitabe mpaka pano, pakati pa Israele ndiponso pakati pa anthu onse. Motero mwatchukitsa dzina lanu mpaka lero lino. Inu ndi dzanja lanu lamphamvu kwambiri mudatulutsadi anthu anu Aisraele ku Ejipito pochita zizindikiro zozizwitsa ndi ntchito zododometsa zimene zidaopsa adani athu. Mudaŵapatsa dziko lino, limene mudalonjeza makolo ao molumbira, dziko lamwanaalirenji. Adaloŵa nkulilanda kuti likhale lao. Koma iwo sadakumvereni, sadatsate malamulo anu. Sankachita zimene mudaaŵalamula. Nchifukwa chake mwaŵagwetsera mavuto onseŵa. Onani, adani akuzinga ndi nthumbira zankhondo mzindawu kuti aulande. Mzinda umenewu udzaperekedwa kwa Ababiloni utafooka ndi nkhondo, njala ndi mliri. Zimene munkanena zija zachitikadi, monga mwadziwonera nokha. Komabe ngakhale mzindawu udzaperekedwa kwa Ababiloni, Inu Chauta mudandilamula kuti ndigule mundawo pali mboni ziŵiri.” Chauta adauza Yeremiya kuti, “Ine ndine Chauta, Mulungu wa anthu onse. Kodi chilipo choti Ine nkundikanika? Nchifukwa chake Ineyo ndikunena kuti ndidzapereka mzindawu kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni. Iyeyo adzaulanda, ndipo Ababiloni amene akuuthira nkhondo, adzaloŵamo. Adzautentha ndi kugwetsa makamaka nyumba zimene padenga pake anthu ankandipsetsa mtima pofukizapo lubani kwa Baala ndi poperekapo chopereka cha chakumwa kwa milungu ina. Chiyambire pa ubwana wao, Aisraele ndi Ayuda akhala akungochita zoipa pamaso panga, nkumandikwiyitsa ndi ntchito zao zoipa,” akutero Chauta. “Mzinda umenewu wakhala ukuutsa mkwiyo wanga ndi ukali wanga kuyambira nthaŵi imene adaumanga mpaka lero lino. Nchifukwa chake ndiyenera kuuchotsa pamaso panga. Aisraele ndi Ayuda, mafumu ao, akalonga, ansembe, aneneri, pamodzi ndi onse okhala ku Yerusalemu ndi ku Yuda, adandikwiyitsa ndi ntchito zao zoipa. Andifulatira kotheratu. Ngakhale ndidavutikira kumaŵaphunzitsa, sadamve kapena kutolapo nzeru iliyonse. Adaika mafano ao onyansa m'Nyumba imene imadziŵika ndi dzina langa, ndipo adaiipitsa. Adamanga nsanja yopembedzerapo Baala m'chigwa cha Benihinomu, kuti apereke ana ao aamuna ndi aakazi ngati nsembe kwa Moleki. Sindidalamule zimenezo ndine, ndipo sindidaganizeko kuti iwo nkuchita zonyansa zoterezi, ndi kuchimwitsa anthu a ku Yuda pakutero.” Anthu ponena za mzinda umenewu akuti udzaperekedwa kwa mfumu ya ku Babiloni utafooka ndi nkhondo, njala ndi mliri. Komatu zimene Chauta, Mulungu wa Israele akunena ndi izi: Akuti, “Ine ndidzaŵasonkhanitsa anthuŵa kuchokera ku maiko onse kumene ndidaŵapirikitsira ndili wokwiya, waukali ndi wopsa mtima kwambiri. Ndidzaŵabwezanso ku malo ano, ndipo adzakhala kuno ndi mtendere wonse. Adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao. Ndidzaŵapatsa mtima umodzi ndi mkhalidwe umodzi, kotero kuti azidzandiwopa nthaŵi zonse. Motero iwowo ndi ana ao omwe, zinthu zidzaŵayendera bwino. Ndidzachita nawo chipangano chosatha. Sindidzaleka kuŵachitira zabwino. Ndidzaŵapatsa mtima wondiwopa, motero sadzandisiyanso. Ndidzakondwera kuŵachitira zabwino. Ndipo ndidzaŵakhazikitsa m'dziko lino mokhulupirika ndi mtima wanga wonse ndi kufuna kwanga konse.” Chauta akunena kuti, “Monga momwe ndidaŵaonongera anthuŵa, momwemonso ndidzaŵapatsa mtendere umene ndidzaŵalonjeza. Anthu adzagulanso minda m'dziko lino limene inu mumati nlosiyidwa, lopanda munthu ndi nyama yomwe, chifukwa adalipereka kwa Ababiloni. Anthu adzaguladi minda ndi ndalama. Mapangano ake adzalembedwa, adzamatidwa ndipo padzakhala umboni wake ku dera la Benjamini, ku malo oyandikana ndi Yerusalemu, m'mizinda ya ku Yuda, m'mizinda yakumapiri, m'mizinda yakuchigwa ndi yakumwera ku Negebu. Zoona, ndidzaŵabwezera ufulu wao,” akuterotu Chauta. Chauta adalankhulanso ndi Yeremiya kachiŵiri, akadali m'ndende m'bwalo la alonda a mfumu, adati, “Naŵa mau a Chauta amene adalenga dziko lapansi, naliwumba ndi kulikhazikitsa. Iyeyo dzina lakedi ndi Chauta. Akuti: Unditame mopemba, ndipo ndidzakuyankha. Ndidzakuuza zinsinsi zazikulu zimene suzidziŵa. Chauta, Mulungu wa Israele, akunenapo mau pa za nyumba za mu mzinda uno ndi za nyumba za mafumu a ku Yuda, zimene anthu adazigwetsa kuti amange zotchinjiriza mzindawo, nthaŵi ya nkhondo. Akuti, Ababiloni akubwera kudzauthira nkhondo, ndipo nyumba zake zidzadzaza ndi mitembo ya anthu amene ndidzaŵapha mokwiya ndi mwachipseramtima. Mzinda umenewu ndaufulatira chifukwa cha makhalidwe oipa a anthu ake. “Komabe m'tsogolo mwake ndidzaupatsanso moyo ndi kuuchiritsa. Anthu ake ndidzaŵachiritsa ndi kuŵapatsa zabwino zochuluka ndi mtendere weniweni. Ndidzakhazikanso pabwino anthu a ku Yuda ndi a ku Israele, ndi kuŵabwezera momwe adaaliri poyamba. Ndidzaŵayeretsa pochotsa machimo ao onse ondichimwira. Ndidzaŵakhululukira zoipa zonse zimene adachita pondipandukira. Mzinda umenewu udzamveketsa mbiri yanga yabwino, ndipo udzandipatsa chimwemwe, chiyamiko ndi ulemu. Anthu a mitundu yonse pansi pano adzanditamanda ndi kundilemekeza pakumva za zabwino zonse zimene ndauchitira mzinda umenewu. Adzachita mantha ndi kunjenjemera, poona kuti mzindawo ndaupatsa madalitso ndi zokoma zosaŵerengeka.” Chauta akuti, “Anthu amanena za malo ano kuti ndi bwinja, opanda munthu ndi nyama yomwe. Komabe m'mizinda ya Yuda ndi m'miseu ya Yerusalemu m'mene tsopano muli zii, mopanda munthu ndi nyama yomwe, mudzamveka mau achisangalalo ndi achimwemwe, mau achikondwerero a mkwati wamwamuna ndi wamkazi. M'Nyumba ya Mulungunso mudzamveka nyimbo ya anthu odzapereka nsembe zothokozera Mulungu. Nyimbo yake azidzati, “ ‘Tamandani Chauta Wamphamvuzonse, popeza kuti ndi wabwino ndipo chikondi chake nchamuyaya!’ Ndithudi, ndidzaŵabwezeranso pabwino monga momwe adaaliri,” akutero Chauta. Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Ku malo ano a chipululu opanda munthu ndi nyama yomwe, ndi ku mizinda yake yonse, kudzakhalanso mabusa kumene abusa angaŵetereko nkhosa zao. Ku mizinda yakumapiri, ku chigwa, kumwera ku Negebu, ku dera la Benjamini, ku maiko oyandikana ndi Yerusalemu ndiponso ku mizinda ya Yuda, nkhosa zidzapitanso pamaso pa munthu woziŵerenga,” akutero Chauta. Chauta akutinso, “Akubwera masiku pamene ndidzachitadi zimene ndidalonjeza anthu a ku Israele ndi a ku Yuda. Masiku amenewo ndiponso pa nthaŵi yomweyo, ndidzaphukitsa nthambi yolungama kuchokera kubanja kwa Davide. Munthuyo adzachita zabwino ndi zolungama m'dziko lonse. Nthaŵi imeneyo anthu a ku Yuda adzapulumuka, ndipo a ku Yerusalemu adzakhala pa mtendere. Motero mzindawu udzakhala ndi dzina loti ‘Chauta ndiye chipulumutso chathu.’ ” Zoonadi, Chauta akunena kuti, “Davide sadzasoŵa mdzukulu woloŵa m'malo mwake pa mpando waufumu wa Israele. Ansembe Achilevi sadzasoŵa munthu womabwera kwa Ine nthaŵi zonse kudzapereka nsembe zopsereza, nsembe zaufa ndi nsembe zinanso, mpaka muyaya.” Chauta adauza Yeremiya kuti, “Mau anga ndi aŵa: Ine ndidachita chipangano ndi usana ndi usiku kotero kuti ziŵirizi zimafika pa nthaŵi yake. Ndipo chipanganocho sichingaphwanyike konse. Chimodzimodzinso ndidachita chipangano ndi Davide, mtumiki wanga, kuti nthaŵi zonse adzakhala ndi mdzukulu wodzakhala pa mpando wake waufumu. Ndidachitanso chipangano china ndi ansembe Achilevi kuti iwowo adzanditumikira nthaŵi zonse. Ndipo zipangano zimenezi sizingaphwanyike konse. Ndidzachulukitsa zidzukulu za mtumiki wanga Davide ndi atumiki anga ansembe Achilevi, kuchuluka kwake ngati kwa nyenyezi zakuthambo kapena kwa mchenga wa m'mphepete mwa nyanja.” Chauta adafunsa Yeremiya kuti, “Kodi sudamve m'mene anthu ena akulankhulira, kumanena kuti, ‘Chauta wakana mabanja aŵiri aja amene adaŵasankha?’ Motero anthuwo amanyoza mpingo wanga osauyesanso ngati mtundu wa anthu. Koma Ine Chauta ndidachita chipangano ndi usana ndi usiku, ndipo ndidapanga malamulo oyendetsa zonse za pa dziko lapansi ndi zamumlengalenga. Tsono monga ndachita zimenezi motsimikiza, chonchonso ndidzachisunga chipangano chimene ndidachita ndi zidzukulu za Yakobe, ndiponso ndi Davide, mtumiki wanga. Ndidzasankhula mmodzi mwa zidzukulu za Davide kuti azilamulira zidzukulu za Abrahamu, Isaki ndi Yakobe. Komatu tsono ndidzaŵamvera chifundo ndi kuŵabwezeranso pabwino.” Inalipo nthaŵi pamene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni ndi gulu lake lankhondo, pamodzi ndi maufumu onse a pa dziko lapansi amene ankaŵalamulira, ndiponso anthu a mitundu yonse, ankathira nkhondo Yerusalemu ndi mizinda yake yozungulira. Nthaŵi imeneyo Chauta adauza Yeremiya kuti, “Pita ukauze Zedekiya mfumu ya ku Yuda kuti Chauta akunena kuti Mzinda uwu ndidzaupereka kwa mfumu ya ku Babiloni, ndipo iyeyo adzautentha. Iweyo sudzapulumuka m'manja mwake. Udzagwidwa ndithu ndipo adzakupereka m'manja mwake. Udzamuwona maso ndi maso, ndipo udzalankhula naye pakamwa ndi pakamwa. Tsono adzakutenga kupita nawe ku Babiloni. Komabe imva mau a Chauta, iwe Zedekiya mfumu ya ku Yuda. Akuti, Sudzafera pa nkhondo. Koma udzafera pa mtendere. Ndipo paja anthu ankafukiza lubani poika maliro a makolo ako akale, amene anali mafumu iweyo usanaloŵe ufumu, tsono nawenso podzaika maliro ako adzafukiza lubani. Pokuimbira nyimbo yamaliro azidzati, ‘Ogo nanu! Mbuyathu uja!’ Ndalankhula zimenezi ndine Mwiniwakene,” akuterotu Chauta. Tsono zonsezi mneneri Yeremiya adakakambira Zedekiya, mfumu ya ku Yuda ku Yerusalemu. Nthaŵi imeneyo nkuti gulu lankhondo la mfumu ya ku Babiloni likuthira nkhondo Yerusalemu ndi mizinda yotsala ya ku Yuda, Lakisi ndi Azeka. Imeneyi yokha ndiyo inali mizinda yamalinga yotsala ya ku Yuda. Mau a Chauta adamvekanso kwa Yeremiya. Nthaŵiyo nkuti mfumu Zedekiya atapangana nawo anthu onse a ku Yerusalemu kuti alengeze zakuti akapolo ao adzaŵamasule. Onse amene anali ndi akapolo Achihebri, aamuna kapena aakazi, aŵamasuledi. Sankayenera kumsunga mu ukapolo Myuda mnzao. Akulu onse pamodzi ndi anthu wamba, atachita chipangano kuti akapolo aŵamasule, kuti asaŵasungenso mu ukapolo, zimenezi zidachitikadi ndipo adaŵamasula. Komabe pambuyo pake adasintha maganizo ao. Amuna ndi akazi amene adaaŵamasula aja, adaŵagwiranso ukapolo. Tsono Chauta adauza Yeremiya kuti akalengeze kwa anthu mau a Chauta akuti, “Ndidachita chipangano ndi makolo anu pa tsiku limene ndidaŵatulutsa ku dziko la Ejipito ku nyumba ya ukapolo ija. Chipanganocho chidati: Zaka zisanu ndi ziŵiri zitatha, aliyense mwa inu ammasule mu ukapolo Muhebri aliyense amene adadzigulitsa kwa inu nagwira ntchito zaka zisanu ndi chimodzi. Koma makolo anu sadandimve ndipo sadasamaleko konse. Komabe masiku omwe apitaŵa mudatembenuka mtima ndipo nkuyamba kuchita zomwe ndimafuna Ine. Nonse mudamvana zoŵapatsa ufulu Aisraele anzanu. M'Nyumba imene imadziŵika ndi dzina langa mudalonjeza kuti mudzachitadi zimenezi. Koma tsono mudasinthanso maganizo, ndipo mwaipitsa dzina langa. Nonsenu mudaŵagwiranso anthu amene mudaaŵamasula aja, nkuŵasandutsanso akapolo anu.” Nchifukwa chake Chauta akunena kuti, “Simudandimvere, simudalengeze ufulu kuti mumasule abale ndi anansi anu. Chabwino! Ineyo tsono ndidzalengeza ufulu wina kwa inu, ufulu wake wa kufa ndi lupanga, mliri kapena njala. Ndidzakusandutsani chinthu chochititsa mantha pakati pa maufumu a pa dziko lapansi. Simudasamale chipangano chimene mudachita ndi Ine, ndipo simudasunge lonjezo limene mudachita pamaso panga. Tsono Ine ndidzakusandutsani ngati mwanawang'ombe uja amene ankamdula paŵiri napita pakati pa zigawozo. Amene ankadutsa pakati pa zigawo ziŵiriwo anali akulu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu, atsogoleri a boma, ansembe, ndiponso anthu a m'dzikomo. Onsewo ndidzaŵapereka kwa adani ao ndi kwa amene amafuna kuŵapha. Ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame ndi nyama zakuthengo. Ndidzapereka Zedekiya, mfumu ya ku Yuda, pamodzi ndi nduna zake, kwa adani ao amene amafuna kuŵapha, ndiye kuti kwa gulu lankhondo la mfumu ya ku Babiloni limene nthaŵi ino layamba kubwerera m'mbuyo. Koma ndidzaŵalamula, ndidzaŵabwezeranso ku mzinda uno. Adzauthira nkhondo ndi kuulanda, ndipo adzautentha. Motero mizinda ya Yuda ndidzaisandutsa chipululu, mopanda anthu.” Pa nthaŵi imene Yehoyakimu, mwana wa Yosiya, anali mfumu ya ku Yuda, Chauta adalankhula nane ine Yeremiya. Adati, “Pita ku banja la Arekabu, ukaŵaitane anthu akumeneko kuti abwere m'chipinda chimodzi cha Nyumba ya Chauta. Atafika, uŵapatse vinyo kuti amwe.” Motero ndidabwera ndi Yazaniya (mwana wa Yeremiya winanso, mwana wa Habaziniya,) pamodzi ndi abale ake ndiponso ana ake onse aamuna, ndiye kuti banja lonse la Arekabu. Ndidabwera nawo ku nyumba ya Chauta, ku chipinda cha ophunzira a Hanani, mwana wa Igadaliya, munthu womvera Mulungu. Chipinda chimenechi chinali pafupi ndi chipinda cha akuluakulu, pamwamba pa chipinda cha Maseiya, mwana wa Salumu, mlonda wapakhomo. Tsono ndidaika mbiya zodzaza ndi vinyo ndi zikho zomwera pamaso pa Arekabuwo, ndipo ndidaŵauza kuti, “Nayu vinyo, imwani.” Koma iwowo adati, “Ife sitimwa vinyoyu, poti kholo lathu Yonadabu mwana wa Rekabu adatilamula kuti, ‘Musadzamwe vinyo, inuyo ndi ana anu omwe. Musadzamange nyumba kapena kubzala mbeu, kapena kulima minda yamphesa. Zinthu zimenezi musadzakhale nazo. M'malo mwake muzidzangokhala m'mahema pa moyo wanu wonse, kuti mukhale nthaŵi yaikulu m'dziko limene mukukhalamo.’ Takhala tikutsata malamulo a kholo lathu Yonadabu, mwana wa Rekabu, ndipo pa moyo wathu wonse sitidamwe vinyo ifeyo, akazi athu, ana athu aamuna ndi ana athu aakazi. Sitidamange nyumba kuti tizikhalamo, kapena kulima minda yamphesa kapena minda ina iliyonse. Tangokhala m'mahema basi. Motero tamvera ndi kusunga malamulo onse a kholo lathu Yonadabu. Koma pamene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adathira nkhondo dziko lino, tidanena kuti, ‘Tiyeni tichoke, tipite ku Yerusalemu kuti tithaŵe magulu ankhondo a Ababiloni ndi a Asiriya.’ Nchifukwa chake tikukhala kuno ku Yerusalemu.” Tsono mau a Chauta adadza kwa Yeremiya onena kuti, Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele akuti, “Pita ukafunse anthu a ku Yuda ndi anthu a ku Yerusalemu kuti, ‘Kodi simungatengeko nzeru ndi kumvera mau anga?’ Lamulo la Yonadabu, mwana wa Rekabu, limene adalamula zidzukulu zake kuti asadzamwe vinyo, iwowo asungadi. Samwa vinyo mpaka lero lino chifukwa chomvera lamulo la kholo lao. Ndakhala ndikulankhula nanu kaŵirikaŵiri kukuchenjezani, komabe simudandimvere. Ndidatuma atumiki anga aneneri kuti adzakuuzeni kuti, ‘Aliyense mwa inu asiye ntchito zake zoipa. Konzani makhalidwe anu, ndipo muleke kutsata milungu ina, musamaipembedza. Motero mudzakhala m'dziko limene ndakupatsani inu ndi makolo anu.’ Komabe inu simudalabadeko, simudandimvere. Ana a Yonadabu, mwana wa Rekabu, adatsata lamulo limene kholo lao lidaŵapatsa. Koma inuyo simudandimvere ai. Nchifukwa chake Ine Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, ndikuti ndidzaŵaononga Ayuda ndi anthu onse okhala ku Yerusalemu, chifukwa chakuti sadandimvere pamene ndidaŵalankhula, sadandiyankhe nditaŵaitana.” Yeremiya adauza Arekabu aja mau a Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akuti, “Chifukwa chakuti mudamvera lamulo la Yonadabu kholo lanu, ndipo mudatsata malangizo ake ndi kuchita zonse zimene adakuuzani kuti muchite, tsono Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, ‘Yonadabu mwana wa Rekabu sadzasoŵa mdzukulu wonditumikira mpaka muyaya.’ ” Chaka chachinai cha ufumu wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya ku Yuda, Chauta adauza Yeremiya kuti, “Tenga buku ndipo ulembepo mau onse amene ndalankhula nawe za Israele ndi Yuda ndi za mitundu yonse ya anthu, kuyambira tsiku limene ndidalankhula nawe nthaŵi ya Yosiya mpaka lero lino. Mwina mwake banja la Yuda lidzamva za zoopsa zonse zimene ndikuti ndiŵagwetsere. Choncho munthu aliyense adzasiya makhalidwe ake oipa. Motero ndidzaŵakhululukira zolakwa zao ndi machimo ao.” Tsono Yeremiya adaitana Baruki mwana wa Neriya. Ndipo Barukiyo adalemba m'bukumo mau onse amene Yeremiya ankamuuza, ndiye kuti mau onse amene Chauta adalankhula ndi Yeremiyayo. Adauza Baruki kuti, “Ine andiletsa kupita ku Nyumba ya Chauta. Ndiye tsono upite ndiwe kumeneko m'malo mwanga pa tsiku losala chakudya, ukaŵerenge mau a Chauta amene ndidakulembetsa m'bukumu, anthu onse alikumva. Udzaŵaŵerenge kwa anthu onse a ku Yuda amene abwera kuchokera ku mizinda yao. Tsono mwina mwake adzapemba kwa Chauta, ndipo munthu aliyense adzasiya makhalidwe ake oipa. Ndithu Chauta waŵakwiyira anthu ameneŵa, ukali wake ndi woyaka kwabasi.” Motero Baruki mwana wa Neriya adachita zonse zimene mneneri Yeremiya adamuuza kuti achite. Adaŵerenga mau a Chauta olembedwa m'buku aja m'Nyumba ya Chauta. Pa mwezi wachisanu ndi chinai wa chaka chachisanu cha ufumu wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda, anthu onse a ku Yerusalemu ndi onse amene adaabwera kumeneko kuchokera ku mizinda ya Yuda, adapangana za kusala chakudya kuti apepese Chauta. Tsono onse ataloŵa m'Nyumba ya Chauta, Baruki adaŵerenga mau a Chauta olembedwa m'buku aja, anthu onse alikumva. Adaŵerengera m'chipinda cha Gemariya, mwana wa mlembi Safani, chimene chinali m'bwalo lapamwamba, pafupi ndi Chipata Chatsopano choloŵera ku Nyumba ya Chauta. Mikaya mwana wa Gemariya, mdzukulu wa Safani, atamva mau onse a Chauta olembedwa m'buku aja, adapita ku nyumba ya mfumu, nakaloŵa m'chipinda cha mlembi. Akuluakulu onse anali atasonkhana m'menemo: mlembi Elisama, Delaya mwana wa Semaya, Elinatani mwana wa Akobori, Gemariya mwana wa Safani, Zedekiya mwana wa Hananiya, pamodzi ndi akuluakulu ena onse. Tsono Mikaya adaŵauza mau onse amene adamva pamene Baruki ankaŵerenga buku anthu alikumva. Pamenepo akuluakulu adatuma Yehudi mwana wa Netaniya, mwana wa Selemiya, mwana wa Kusi, kwa Baruki kukamuuza kuti abwere nalo buku limene ankaŵerengera anthu. Motero Baruki mwana wa Neriya, adapita nalo bukulo kwa iwo. Iwowo adati, “Khala apa, ndipo utiŵerengere.” Baruki adaŵaŵerengeradi. Atamva zimene adaaŵerengazo, adayamba kuyang'anitsitsana ali njenjenje ndi mantha. Tsono adauza Baruki kuti, “Tiyenera kuŵauza amfumu mau onseŵa. Koma tatiwuza, m'mene udalembera mau onseŵa. Kodi ndi Yeremiya adakulembetsa zimenezitu ati?” Baruki adayankha kuti, “Inde, ndi Yeremiyadi amene ankanditchulira mau ameneŵa, ine nkumalemba ndi inki m'buku.” Akuluakulu aja adauza Baruki kuti, “Iweyo ndi Yeremiyayo mukabisale, pasakhale munthu wodziŵa kumene muli.” Tsono iwo adaloŵa m'bwalo napita kwa mfumu ataika bukulo m'chipinda cha mlembi Elisama. Adaiwuza mfumuyo mau onsewo. Mfumu itamva zimenezi, idatuma Yehudi kukatenga buku lija. Atakalitenga ku chipinda cha mlembi Elisama, Yehudi adaŵerengera mfumu ndi akuluakulu onse amene adasonkhana. Unali mwezi wachisanu ndi chinai ndipo mfumu inali m'nyumba ya pa nyengo yachisanu, ikuwotha moto umene ankasonkha chifukwa cha kuzizira. Yehudi ankati akaŵerenga masamba atatu kapena anai a bukulo, mfumu inkaŵagwira nkuŵadula ndi mpeni, niŵaponya m'malaŵi a moto. Idapitirira kuchita zimenezi mpaka buku lonse lidapsa ndi moto. Komabe mfumu kapena wina aliyense mwa aphungu ake amene adamva mau ameneŵa, sadachite mantha kapena kung'amba zovala zao. Ndipo pamene Elinatani, Delaya ndi Gemariya adapempha mfumu kuti isatenthe bukulo, iyoyo sidaŵamvere. Kenaka mfumu idalamula Yerahamele mwana wa mfumu, Seraya mwana wa Aziriele ndi Selemiya mwana wa Abideele kuti akagwire mlembi Baruki ndi mneneri Yeremiya. Koma Chauta anali ataŵabisa. Tsono mfumu itatentha bukulo m'mene munali zonse zimene Yeremiya adaalembetsa Baruki, Chauta adauza Yeremiya kuti, “Tsopano tenga buku lina kuti ulembemo mau onse amene adaali m'buku loyamba, limene Yehoyakimu, mfumu ya ku Yuda, adatentha. Ndipo za Yehoyakimu, mfumu ya ku Yuda, ukamuuze kuti, ‘Chauta akuti, Paja iwe udatentha buku lija, nkumanena kuti, “Chifukwa chiyani walemba kuti mfumu ya ku Babiloni idzafika kudzaononga dziko lino ndi kuwononga anthu ndi nyama zomwe?” Nchifukwa chake za Yehoyakimu, mfumu ya ku Yuda, Chauta akunena kuti sipadzaoneka wina woloŵa m'malo mwake pa mpando waufumu wa Davide. Akadzafa, mtembo wake masana udzakhala pa dzuŵa, ndipo usiku udzakhala pa chisanu. Ndidzamlanga pamodzi ndi zidzukulu zake ndi aphungu ake chifukwa cha zoipa zao. Ndidzaŵagwetsera iwowo ndi anthu onse a ku Yerusalemu ndi a ku Yuda zoopsa zonse zimene ndidanena, chifukwa iwo sadamvere mau anga.’ ” Tsono Yeremiya adatenga buku lina napatsa mlembi Baruki, mwana wa Neriya, namlembetsa mau onse a m'buku limene Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda adatentha lija. Ndipo adaonjezerapo mau ambiri monga omwewo. Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, adakhazika Zedekiya pa mpando waufumu wa ku Yuda, kuloŵa m'malo mwa Yehoyakini mwana wa Yehoyakimu. Koma Zedekiyayo ndi aphungu ake, pamodzi ndi anthu onse a m'dzikomo, sadamvere mau amene Chauta adalankhula kudzera mwa mneneri Yeremiya. Tsono mfumu Zedekiya adatuma Yehukala, mwana wa Semaliya ndi wansembe Zefaniya, mwana wa Maseiya, kwa mneneri Yeremiya kukamuuza kuti, “Mutipempherere kwa Chauta, Mulungu wathu.” Pa nthaŵi imeneyo nkuti Yeremiya asanaponyedwe m'ndende, choncho anali ndi ufulu wotha kuyenda pakati pa anthu. M'menemonso nkuti gulu lankhondo la Farao litatuluka ku Ejipito. Ndipo pamene Ababiloni ozinga mzinda wa Yerusalemu ndi zithando zankhondo adamva zimenezo, adachokako ku Yerusalemuko. Tsono Chauta adauza mneneri Yeremiya kuti, “Ine Chauta, Mulungu wa Israele, ndikunena kuti mfumu ya ku Yuda imene idakutuma kuti udzapemphe nzeru kwa Ine, uiwuze kuti, ‘Gulu lankhondo la Farao limene lidaabwera kuti lidzakuthandize, posachedwa libwerera kwao ku Ejipito, dziko lake. Ndipo Ababiloni adzabwerera kudzathira nkhondo mzinda uno. Adzaugonjetsa ndi kuutentha.’ Zimene akunena Chauta ndi izi, akuti musadzinyenge ndi kumaganiza kuti Ababiloni adzachoka ndi kukusiyani. Pepani sadzachoka ai. Ngakhale mutagonjetsa gulu lonse la Ababiloni limene mukumenyana nalo nkhondo, ngakhalenso mwa iwowo mutatsala ovulala okhaokha m'mahema mwao, iwo omwewo adzadzambatuka nkuutentha mzindawu.” Pamene gulu lankhondo la Ababiloni lidaleka kuthira nkhondo mzinda wa Yerusalemu, chifukwa choopa gulu lankhondo la Farao, Yeremiya adanyamuka kuchoka ku Yerusalemu kupita ku dziko la Benjamini kuti akalandire gawo lake la minda ya makolo ake. Pamene adafika pa Chipata cha Benjamini, mlonda wina wapamenepo, dzina lake Iriya, mwana wa Selemiya, mwana wa Hananiya, adagwira Yeremiya, nati, “Iwetu ukuthaŵira kwa Ababiloni ati!” Yeremiya adati, “Zimenezo ai, si zoona. Ine sindikuthaŵira kwa Ababiloni.” Koma Iriyayo sadamumvere ndipo adamgwira nabwera naye kwa akuluakulu. Akuluakulu aja adamkwiyira Yeremiya. Adamkwapula, namtsekera m'nyumba ya mlembi Yonatani imene adaaisandutsa ndende. Yeremiya adaikidwa m'ndende ya pansi pa nthaka, nakhala m'menemo nthaŵi yaitali. Tsiku lina mfumu idatuma anthu kuti akaitane Yeremiya, ndipo idamlandira. Idamufunsa paseri m'nyumba mwake kuti, “Kodi pali mau amene Chauta wakuuza?” Yeremiya adayankha kuti, “Inde, alipo. Inu amfumu mudzaperekedwa m'manja mwa mfumu ya ku Babiloni.” Ndipo adafunsa mfumu Zedekiya kuti, “Kodi ndakulakwirani chiyani inuyo, aphungu anu, kapena anthu anu kuti mundiponye m'ndende? Kodi ali kuti aneneri anu aja amene adakuloserani kuti mfumu ya ku Babiloni sidzakuthirani nkhondo inuyo ndi dziko lanu? Tsono ndikukupemphani inu mfumu mbuyanga, kuti mumve pempho langa. Musandibwezere ku nyumba ya mlembi Yonatani, kuwopa kuti ndingakafereko.” Pamenepo mfumu Zedekiya adalamula kuti Yeremiya asungidwe ku bwalo la alonda. Tsono ankamupatsa chakudya tsiku ndi tsiku, mtanda umodzi wa buledi. Ankamugula kwa anthu opanga buledi, mpaka buledi yense mumzindamo adatha. Motero Yeremiya adakhala m'bwalo la alonda. Tsono Sefatiya mwana wa Matani, Gedaliya mwana wa Pasuri, Yukala mwana wa Selemiya, ndi Pasuri mwana wa Malakiya, adamva zimene Yeremiya ankauza anthu zoti Chauta akunena kuti, “Aliyense amene atsalire mu mzinda uno adzafa ndi nkhondo, njala ndiponso mliri. Koma aliyense amene atuluke kukadzipereka kwa Ababiloni adzakhala moyo, adzapulumutsa moyo wake. Mzinda uno udzaperekedwadi kwa ankhondo a mfumu ya ku Babiloni, ndipo adzaulanda.” Tsono akuluakulu adauza mfumu kuti, “Munthuyu ayenera kuphedwa. Akutayitsa mtima ankhondo ndi anthu onse otsalira mu mzinda, chifukwa cha zolankhula zakezi. Munthu ameneyu sakuŵafunira zabwino anthu, angofuna kuti aonongedwe basi.” Mfumu Zedekiya adati, “Suyu, ali m'manja mwanu. Ine mfumu sindingakuletseni ai.” Choncho iwo aja adatenga Yeremiya, nakamponya m'chitsime chimene adaakumba Malakiya mwana wa mfumu, m'bwalo la alonda a mfumu. Adamtsitsira m'menemo ndi chingwe. M'chitsimemo munalibe madzi, munali matope okhaokha. Ndipo Yeremiya adamira m'matopemo. Tsono Ebedemeleki, Mkusi wina wofulidwa wogwira ntchito ku nyumba ya mfumu, adamva kuti Yeremiya amponya m'chitsime. Nthaŵi imeneyo nkuti mfumu ili ku Chipata cha Benjamini. Ebedemeleki adatuluka ku nyumba ya mfumu kukaiwuza kuti, “Mfumu mbuyanga, anthu aŵa amchita zoipa kwambiri mneneri Yeremiya. Amponya m'chitsime, ndipo poti buledi adatha mu mzinda, adzafa ndi njala m'menemo.” Tsono mfumu idalamula Mkusi Ebedemeleki kuti, “Tenga anthu atatu, mukamtulutse mneneri Yeremiya asanafe.” Apo Ebedemeleki adapita ku nyumba ya mfumu ndi anthuwo, nakatenga nsanza m'chipinda cha zovala. Nsanzazo adazitsitsa ndi zingwe m'chitsime m'mene munali Yeremiya. Ebedemeleki Mkusi uja adauza Yeremiya kuti, “Ikani nsanzazi m'kwapa mwanu kuti zingwe zingakupwetekeni.” Yeremiya adachitadi zimenezo. Tsono adamtulutsira kunja ndi zingwe, ndipo Yeremiya adakakhalanso konkuja ku bwalo la alonda. Tsiku lina mfumu Zedekiya adaitana mneneri Yeremiya namlandira pa chipata chachitatu cha ku Nyumba ya Chauta. Adamuuza kuti, “Ndifuna kukufunsa kanthu, usati undibisire ai.” Yeremiya adayankha kuti, “Ndikakuuzani, mosapeneka konse mundipha. Ndikakulangizani simumvera.” Apo mwachinsinsi mfumu Zedekiya adalumbira pamaso pa Yeremiya kuti, “Pali Chauta wamoyo amene adatipatsa moyo, ine sindikupha. Ndipo sindikupereka kwa anthu amene afuna kukuphaŵa.” Yeremiya adauza Zedekiya kuti, “Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, ‘Ngati mutuluka kukadzipereka kwa akuluakulu a mfumu ya ku Babiloni, mudzakhala ndi moyo, ndipo mzinda uno sadzautentha. Inuyo pamodzi ndi banja lanu mudzakhala moyo. Koma mukangopanda kudzipereka kwa akuluakulu a mfumu ya ku Babiloni, mzindawu udzaperekedwa m'manja mwa Ababiloni, ndipo adzautentha, tsono inu simudzapulumuka m'manja mwao.’ ” Mfumu Zedekiya adauza Yeremiya kuti, “Ndikuwopa Ayuda amene adathaŵira kale kwa Ababiloni. Ndikuwopa kuti Ababiloni adzandipereka kwa Ayudawo, ndipo iwowo adzandichita zoipa.” Yeremiya adayankha kuti, “Iyai, sadzakuperekani. Ngati mumvera Chauta pa zonse, ndikukuuzani kuti zinthu zonse zidzakuyenderani bwino, ndipo mudzakhala ndi moyo. Koma mukakana kutuluka kuti mukadzipereke, Chauta wandiwululira kuti akazi onse otsala m'nyumba ya mfumu ya ku Yuda, adzaperekedwa kwa akuluakulu a mfumu ya ku Babiloni. Popita ku Babiloniko, akazi amenewo azidzaimba kuti, “ ‘Abwenzi ako okhulupirika aja adakunyenga, ndipo adakugonjetsa. Tsopano poti miyendo yako yazama m'matope, abwenzi akowo akusiya.’ Akazi anu onse pamodzi ndi ana adzaŵapereka m'manja mwa Ababiloni. Ndipo inuinuyo simudzalephera kugwa m'manja mwao. Mudzagwidwa ndi mfumu ya ku Babiloni, kenaka mzinda uno adzautentha.” Pamenepo Zedekiya adauza Yeremiya kuti, “Usauze munthu wina aliyensetu zimenezi, kuti ungaphedwe. Akuluakulu akamva kuti ndakhala ndikulankhula nawe, makamaka abwera kwa iwe kudzanena kuti, ‘Utiwuze zimene wauza amfumu, ndi zimene iwowo akuuza, usatibisire, ndipo sitidzakupha.’ Tsono udzaŵayankhe kuti, ‘Ndinalikupempha kwa amfumu kuti asandibwezenso ku nyumba ya Yonatani, kuti ndikafe kumeneko.’ ” Akuluakulu onse adabweradi kwa Yeremiya kudzamufunsa. Iye adaŵayankha monga momwe mfumu idamuuzira. Motero nkhani zao zidathera pomwepo, chifukwa mau aja anali asanamveke kwa munthu wina aliyense. Tsono Yeremiya adakhalabe m'bwalo la alonda, mpaka tsiku limene mzinda wa Yerusalemu udagonjetsedwa. Pa chaka chachisanu ndi chinai cha ufumu wa Zedekiya ku Yuda, mwezi wakhumi, Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, adadza ndi gulu lake lonse lankhondo ku Yerusalemu, nazinga mzindawo. Pa chaka chakhumi ndi chimodzi cha ufumu wa Zedekiya, mwezi wachinai, tsiku lachisanu ndi chinai la mweziwo, malinga a mzindawo adabooledwa. Pamenepo akuluakulu onse a mfumu ya ku Babiloni adaloŵa nakakhala pa chipata chapakati. Anali aŵa: Neregali-Sarezere, Samugiri-Nebo, Sarisekimu mkulu wa nduna, ndi Neregali-Sarezere winanso mkulu wolamulira gulu lankhondo lapatsogolo, pamodzi ndi akuluakulu ena onse a mfumu ya ku Babiloni. Pamene Zedekiya, mfumu ya ku Yuda, adaŵaona, iyeyo pamodzi ndi ankhondo ake adathaŵa mumzindamo usiku, kudzera ku munda wa mfumu, kubzola pa chipata cha pakati pa zipupa ziŵiri. Adathaŵira ku Araba. Koma gulu lankhondo la Ababiloni lidamlondola ndi kukamgwira Zedekiyayo ku zigwa za ku Yeriko. Mfumuyo ataigwira, adapita nayo kwa Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, ku Ribula m'dziko la Hamati. Ndipo adagamula mlandu wake komweko. Tsono mfumu ya ku Babiloni idapha ana aamuna a Zedekiya ku Ribula, iyeyo akuwona. Idaphanso atsogoleri onse a ku Yuda. Kenaka idamkolowola maso Zedekiyayo, nimmanga ndi maunyolo nkupita naye ku Babiloni. Ababiloni adatentha nyumba yaufumu, Nyumba ya Chauta pamodzi ndi nyumba zina zonse za anthu. Ndipo adagwetsa malinga a Yerusalemu. Nebuzaradani, mtsogoleri wa alonda ankhondo, adatenga anthu onse otsala a mumzindawo kupita nawo ku Babiloni. Ameneŵa ndiwo amene adaadzipereka kwa iye, ndiponso anthu amene adaatsalira. Nebuzaradani, mtsogoleri wa alonda ankhondoyo, adasiya anthu okhaokha osauka kwambiri, ndi opanda nkanthu komwe m'dziko la Yuda. Ndipo adaŵapatsa minda yamphesa ndi minda inanso. Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, adatumiza mau kwa Nebuzaradani mtsogoleri wa alonda ankhondo, onena za Yeremiya. Adati, “Mtenge, umsamale bwino, usamvute, koma umchitire zimene afuna.” Motero Nebuzaradani, mtsogoleri wa alonda ankhondo uja, adanyamuka pamodzi ndi Nebusazibani mtsogoleri wamkulu, Neregali-Sarezere mkulu wolamulira gulu lankhondo linanso ndi akuluakulu onse a mfumu ya ku Babiloni. Iwowo adakatenga Yeremiya ku bwalo la alonda, nakampereka kwa Gedaliya, mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani, kuti amumasule ndi kumtumiza kunyumba kwake. Motero Yeremiya adakakhala ndi anthu ake. Chauta adalankhula ndi Yeremiya pamene anali m'ndende ku bwalo la alonda. Adati, “Pita ukauze Ebedemeleki Mkusi uja kuti Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele akunena kuti, ‘Zidzachitikadi zimene ndidaanena za mzinda uno, ndipo nzoipa osati zabwino, ai. Zidzachitikadi pa nthaŵi yake, iwe ukupenya. Iweyo ndidzakupulumutsa tsiku limenelo, ndipo sudzaperekedwa kwa anthu amene umaŵaopa. Ndithu ndidzakupulumutsa, ndipo sudzaphedwa pa nkhondo. Udzapulumuka chifukwa choti wandikhulupirira,’ ” akuterotu Chauta. Chauta adalankhula ndi Yeremiya pa nthaŵi imene Nebuzaradani mtsogoleri wa alonda ankhondo adammasula ku Rama. Adaampeza ali womangidwa ndi unyolo pamodzi ndi am'ndende ena a ku Yerusalemu ndi a ku Yuda opita nawo ku Babiloni. Mtsogoleriyo adatenga Yeremiya namuuza kuti, “Chauta, Mulungu wako, adanena kuti adzaononga malo ano. Ndipo zimenezi wazichitadi monga momwe adaanenera, chifukwa chakuti inu anthu mudachimwira Chauta, simudamumvere. Koma iwe Yeremiya, lero ndikukumasula maunyolo m'manjamu. Tiye ku Babiloni ngati ufuna, ndipo ndidzakusamala bwino. Koma ngati sufuna kupita, palibe kanthu. Dziko ndi lonseli monga ukuwonera, upite kumene uwona kuti nkoyenera. Ngati supita, ubwerere kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani amene mfumu ya ku Babiloni idaamsankha kuti akhale bwanamkubwa wa mizinda ya ku Yuda. Ukakhale ndi iyeyo pakati pa anthu, kapena upite kulikonse kumene ufuna.” Tsono mtsogoleri wa nkhondo uja adampatsa chakudya, nampatsanso mphatso, ndipo adamuuza kuti, “Ai, pita bwino!” Pamenepo Yeremiya adapita kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa. Ndipo adakhala naye pakati pa anthu otsala m'dzikomo. Panali atsogoleri ena ankhondo amene sadadzipereke nao. Iwowo pamodzi ndi anthu ao adamva kuti mfumu ya ku Babiloni idaika Gedaliya, mwana wa Ahikamu, kuti akhale bwanamkubwa wa dzikolo, aziyang'anira anthu osauka kwambiri aja, amuna, akazi ndi ana, amene sadaŵatenge ukapolo kupita nawo ku Babiloni. Tsono amene adapita kwa iye ku Mizipa ndi aŵa: Ismaele mwana wa Netaniya, Yohanani ndi Yonatani ana a Kareya, Seraya mwana wa Tanihumeti, ana aamuna a Efayi a ku Netofa, ndi Yezaniya mwana wa Maaka, iwowo pamodzi ndi anthu ao. Onsewo, Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani, adaŵalonjeza molumbira kuti, “Musaope kuŵagwirira ntchito Ababiloniwo. Khalani m'dzikomu, muzimera mfumu ya ku Babiloni, ndipo zinthu zonse zidzakuyenderani bwino. Ine nditsalira ku Mizipa kuti ndizikuimirirani kwa Ababiloni akamabwera. Koma inu mutenge zipatso zanu, vinyo wanu, mafuta anu, ndipo muzisunge ndithu. Muzikhala m'mizinda imene mwalandayo.” Nawonso Ayuda a ku Mowabu, ku Amoni ndi ku Edomu ndi a ku maiko ena, adamva kuti mfumu ya ku Babiloni idasiyako anthu ena ku Yuda, ndipo kuti idaŵaikira Gedaliya, mwana wa Ahikamu mdzukulu wa Safani, kuti akhale bwanamkubwa wao. Tsono Ayuda onsewo adabwera kuchokera ku maiko onse kumene adaabalalikira. Adabwerera ku Yuda nakadziwonetsa kwa Gedaliya ku Mizipa. Ndipo minda yao idabereka zipatso zambiri ndi vinyo wambiri. Tsiku lina Yohanani mwana wa Kareya, pamodzi ndi atsogoleri ankhondo amene sadadzipereke aja, adapita kwa Gedaliya ku Mizipa. Adamufunsa kuti, “Kodi mukudziŵa kuti Baalisi mfumu ya Aamoni watuma Ismaele, mwana wa Netaniya kuti adzakupheni?” Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu sadaŵakhulupirire. Tsono Yohanani mwana wa Kareya, mwachinsinsi adauza Gedaliya kuti, “Loleni kuti ndikaphe Ismaele mwana wa Netaniyayu, ndipo wina aliyense sadzadziŵa. Nanga inu akuphereninji ndi kulola kuti Ayuda onse okuzunguliraniŵa amwazikane, ndipo otsala a ku Yuda adzaonongedwe?” Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu adayankha Yohanani mwana wa Kareya kuti, “Iyai, usachite zotero. Zimene ukunena za Ismaele nzabodza.” Pa mwezi wachisanu ndi chiŵiri, Ismaele mwana wa Netaniya, mdzukulu wa Elisama, wa m'banja la mfumu, mmodzi mwa atsogoleri akuluakulu a mfumu, adafika ndi anthu khumi ku Mizipa kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu. Pamene ankadya naye kumeneko, Ismaele, mwana wa Netaniya, pamodzi ndi anthu khumi aja, adadzambatuka napha Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani. Adamupha ndi malupanga ao munthu amene mfumu ya ku Babiloni idaamuika kuti akhale bwanamkubwa wa dziko. Ismaele adaphanso Ayuda onse amene anali ku Mizipa ndiponso ankhondo a Ababiloni amene anali kumeneko. M'maŵa mwake, anthu asanadziŵe kuti Gedaliya waphedwa, kudafika anthu makumi asanu ndi atatu kuchokera ku Sekemu, ku Silo ndi ku Samariya. Ndevu zao adaameta, zovala zao zinali zong'ambikang'ambika, ndipo matupi ao anali otemekatemeka. Adatenga nsembe zaufa ndi lubani, kukapereka ku Nyumba ya Chauta. Tsono Ismaele, mwana wa Netaniya, adabwera akulira kuchokera ku Mizipa kudzakumana nawo. Atakumana nawo, adati, “Bwerani, mudzaonane ndi Gedaliya mwana wa Ahikamu.” Atangofika pakati pa mudzi, Ismaele mwana wa Netaniya ndi anthu ake, adaŵapha onsewo naŵataya m'chitsime. Koma pa gulu limenelo panali anthu khumi amene adaauza Ismaele kuti, “Ifeyo musatiphe, tili ndi tirigu, barele, mafuta, ndi uchi, zimene tidabisa m'minda.” Motero adaŵaleka osaŵaphera kumodzi ndi anzao aja. Chitsime chimene Ismaele adatayamo anthu amene adaŵapha aja chinali chitsime chachikulu chija chimene adaakumba ndi mfumu Asa, ataopsedwa ndi Basa mfumu ya ku Israele. Ismaele, mwana wa Netaniya adachidzaza ndi mitembo. Pambuyo pake Ismaele adaŵatenga ukapolo anthu onse amene adatsala ku Mizipa. Anthuwo ndi aŵa: ana aakazi a mfumu, ndi onse otsala ku Mizipa, amene Nebuzaradani mtsogoleri wa nkhondo adaŵapatsa Gedaliya mwana wa Ahikamu kuti akhale bwanamkubwa wao. Ndipo anthu ameneŵa adachoka nawo ndi cholinga choti akaloŵe nawo m'dziko la Aamoni. Pamene Yohanani, mwana wa Kareya, ndi atsogoleri a ankhondo, adamva zoipa zimene Ismaele mwana wa Netaniya adaachita, adasonkhanitsa anthu onse amene anali nawo, napita kukamenyana naye nkhondo. Adakampeza ku chidziŵe cha ku Gibiyoni. Ndipo anthu onse amene Ismaele adaaŵagwira ataona Yohanani mwana wa Kareya ndi atsogoleri a magulu ankhondo aja, adasangalala. Anthu onse amene Ismaele adaaŵatenga ukapolo kuchoka nawo ku Mizipa, adabwerera napita kwa Yohanani mwana wa Kareya. Koma Ismaele mwana wa Netaniya, pamodzi ndi anthu ake asanu ndi atatu, adathaŵa Yohanani, kuthaŵira kwa Aamoni. Pamenepo Yohanani mwana wa Kareya pamodzi ndi atsogoleri a magulu ankhondo, adatenga otsala a ku Mizipa amene Ismaele mwana wa Netaniya, adaaŵatenga ukapolo, atapha Gedaliya mwana wa Ahikamu. Amene adaŵatengawo anali ankhondo, akazi, ana ndi otumikira bwalo la mfumu, amene Yohanani adaabwera nawo kuchokera ku Gibiyoni. Adanyamuka ulendo wao nakaima ku Geruti-Kimuhamu, pafupi ndi Betelehemu. Ankafuna kupita ku Ejipito, chifukwa choopa Ababiloni. Anali ndi manthadi chifukwa choti Ismaele mwana wa Netaniya, adaapha Gedaliya, mwana wa Ahikamu, amene mfumu ya ku Babiloni idaamuika kuti akhale bwanamkubwa wa dziko. Atsogoleri onse a ankhondo, pamodzi ndi Yohanani mwana wa Kareya, Azariya mwana wa Hesaya, kudzanso anthu onse ang'onoang'ono ndi akuluakulu omwe, adapita kwa mneneri Yeremiya. Adamuuza kuti, “Ife tabwera ndi dandaulo lathu. Chonde, mutipempherere kwa Chauta, Mulungu wanu, ife amene tatsala oŵerengeka. Tangotsalatu ochepa chabe pa anthu ambiri, monga mukutiwoneramu. Mupemphere kuti Chauta, Mulungu wanu atiwuze kumene tiyenera kupita ndi zimene tikachite.” Apo mneneri Yeremiya adaŵauza kuti, “Ndamva zimene mwanenazi, ndidzapemphera kwa Chauta, Mulungu wanu monga mukufunira. Ndipo zonse zimene Chauta Mulungu wanu ati anene, ndidzakuuzani, sindidzakubisirani kanthu.” Iwowo adauza Yeremiya kuti, “Chauta akhale mboni yoona ndi yokhulupirika yodzatitsutsa ngati sitichita zimene Chauta Mulungu wanu wakutumani kuti mudzatiwuze. Kaya nzabwino, kaya zoipa, tidzamvera ndithu mau a Chauta Mulungu wathu, amene takutumani kuti mukampemphe kanthu m'dzina lathu. Tidzamvera Chauta Mulungu wathu, kuti zinthu zitiyendere bwino.” Atatha masiku khumi, Chauta adalankhula ndi Yeremiya. Tsono Yeremiya adaitana Yohanani mwana wa Kareya, pamodzi ndi atsogoleri onse a ankhondo amene anali nawo, ndiponso anthu onse, ang'onoang'ono ndi akuluakulu omwe. Adaŵauza kuti, “Chauta, Mulungu wa Israele, amene mudaandituma kuti ndikampemphe kanthu m'dzina lanu, akunena kuti, ‘Ngati mukhala m'dziko lino, ndiye kuti mudzakhazikika, sindidzakuchotsani. Zoonadi, ndidzakukhazikitsani, osakuchotsani konse. Ndikumva chisoni chifukwa cha mazunzo amene ndidagwetsa pa inu. Musaiwope mfumu ya ku Babiloni imene mukuiwopa tsopano. Musaiwope mfumuyo, chifukwa Ine ndili nanu, kuti ndikupulumutseni ndi kukuchotsani m'manja mwake, ndatero Ine Chauta. Ndidzakuchitirani chifundo, kotero kuti iyenso adzakuchitirani chifundo ndi kukulolani kuti mukhale m'dziko lanu lino.’ Koma mwina simumvera mau a Chauta, nkunena kuti, ‘Ai, tipita ndithu ku Ejipitoko, kopanda nkhondo, kosamva kulira kwa lipenga, kosasoŵa chakudya, ndipo tidzakhala kumeneko.’ Tsono mukatero, inu otsala a ku Yuda, imvani mau aŵa a Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele. Akunena kuti, ‘Mukatsimikiza za kupita ku Ejipitozi, nkupitadi kukakhala kumeneko, ndiye kuti nkhondo mukuiwopayo idzakugonjetsani ku Ejipito komweko. Njala mukuiwopayo idzakuvutanibe ngakhale ku Ejipitoko, ndipo mudzafera kumeneko. Anthu onse amene akutsimikiza za kupitadi ku Ejipito, ndi kukakhala kumeneko, adzafa ndi nkhondo, njala ndiponso mliri. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzatsale kapena kupulumuka ku zoopsa zimene ndidzaŵagwetsere.’ ” “Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunenanso kuti, ‘Monga momwe anthu okhala ku Yerusalemu ndidaŵakwiyira mwaukali, momwemonso ndidzakukwiyirani inuyo mukadzapita ku Ejipito. Mudzasanduka chinthu chonyansa ndi chochititsa mantha, chomachiseka ndi chonyozeka. Malo ano simudzaŵaonanso. Inu otsala a ku Yuda, musapite ku Ejipito. Ndithudi ndakuchenjezani lero, kusokera kwanu kungakutayitseni moyo.’ Paja mudaandituma kwa Chauta Mulungu wanu ndi kunena kuti, ‘Mutipempherere kwa Chauta Mulungu wathu, ndipo mutiwuze chilichonse chimene Chauta Mulungu wathu ati anene, ife tidzazichita.’ Ndakuuzani zonse lero, koma simudamvere Chauta Mulungu wanu pa zonse zimene adandituma kuti ndikuuzeni. Tsono mudziŵe kuti mudzafadi ndi nkhondo, njala ndiponso mliri, ku malo amene mufuna kupita kuti mukakhaleko.” Yeremiya atatsiriza kuuza anthu zonse zimene Chauta Mulungu wao adamtuma kuti akaŵauze, Azariya mwana wa Hesaya, Yohanani mwana wa Kareya, ndiponso anthu onse achipongwe, adauza Yeremiya kuti, “Iwe ukunama. Chauta Mulungu wathu sadakutume kudzanena kuti, ‘Musapite ku Ejipito kukakhala kumeneko.’ Baruki mwana wa Neriya ndiye wakukakamiza kuti utiletse, ndipo kuti tigwe m'manja mwa Ababiloni, kuti atiphe kapena kutitenga ukapolo kupita ku Babiloni.” Tsono Yohanani mwana wa Kareya ndi atsogoleri onse a ankhondo, pamodzi ndi anthu onse a ku Yuda, adakana kumvera Chauta ndipo sadakhale ku Yuda. Choncho Yohanani mwana wa Kareya, pamodzi ndi atsogoleri a ankhondo, adatenga anthu onse otsala a ku Yuda amene adabwerera kuchokera ku maiko kumene adaabalalikira kuti akakhale ku Yuda. Anthuwo anali aŵa: amuna, akazi ndi ana, kuphatikizapo ana aakazi a mfumu, ndiponso anthu onse amene Nebuzaradani, mtsogoleri wa ankhondo adaaŵasiya kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani. Adatenganso mneneri Yeremiya ndi Baruki mwana wa Neriya. Onsewo adapita nawo ku Ejipito monyoza mau a Chauta, nakafika ku Tapanesi. Chauta adalankhula ndi Yeremiya ku Tapanesi. Adamuuza kuti, “Tenga miyala ina yaikulu, uikwirire m'dothi pa chiwundo cha poloŵera ku nyumba yaufumu ya Farao ku Tapanesi. Ayuda akuwone ukuchita zimenezo. Tsono uŵauze kuti Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, ‘Ndidzaitana mtumiki wanga Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni. Iyeyo adzaika mpando wake pa miyala imene ndaibisa apoyo. Ndipo adzafunyulula hema lake laufumu pa miyalayo. Adzabwera kudzaononga Ejipito, adzatumiza mliri pa anthu oyenera kufa ndi mliri, adzatenga ukapolo anthu oyenera kutengedwa ukapolo, ndipo adzaŵapha ndi lupanga oyenera kuphedwa ndi lupanga. Adzasonkha moto m'nyumba za milungu ya ku Ejipito. Adzatentha nyumbazo, ndipo milunguyo adzaitenga kupita nayo ku ukapolo. Adzayeretsa dziko la Ejipito monga momwe mbusa amamangira chovala chake m'chiuno, momwemonso ndimo adzaŵachitire Aejiptio ndipo adzachoka ku Ejipito osaona vuto lililonse. Adzaphwanya zipilala zachipembedzo za ku nyumba yopembedzeramo mulungu wa dzuŵa ku Ejipito. Ndipo adzatentha nyumba za milungu ya ku Ejipito.’ ” Nawu uthenga umene Yeremiya adalandira wonena za Ayuda amene ankakhala ku dziko la Ejipito ku Migidoli, ku Tapanesi, ku Memfisi ndi ku dziko la Patirosi: “Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, Mwaziwona zoopsa zimene ndidagwetsa pa Yerusalemu ndi mizinda yonse ya ku Yuda. Tsopano yonseyo yasanduka mabwinja, yopanda anthu okhalamo. Zonsezi zidachitika chifukwa cha machimo a anthu amene adaputa mkwiyo wanga, pofukizira lubani milungu ina ndi kumaitumikira, milungu imene sadaidziŵe iwowo kapena inu kapenanso makolo anu. Komabe ine ndidakhala ndikutuma atumiki anga aneneri kuti adzakuuzeni kuti, ‘Musamachita zoipa zimene Ine ndimadana nazo.’ Koma makolo anuwo sadamvere, sadasamaleko nkomwe. Sadaleke kuchita zoipa zao, sadasiye kuifukizira lubani milungu ina. Motero ukali wa mkwiyo wanga udayaka ngati moto m'mizinda ya ku Yuda ndi ku miseu ya mu Yerusalemu. Mizindayo idasanduka mabwinja osiyidwa, monga m'mene iliri leromu. “Ndiye tsopano Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akuti, Chifukwa chiyani mukuti mudziwononge chotero? Chifukwa chiyani mukufuna kuphetsa Ayuda amuna ndi akazi, ana ndi makanda, osakutsalirani ndi mmodzi yemwe pa mtundu wanu? Chifukwa chiyani mukuputa mkwiyo wanga pochita zoipa ndi manja anu ndiponso pomafukizira lubani milungu ina m'dziko la Ejipito m'mene mukukhala? Mudziwononga nokha, ndipo musanduka chinthu chomachiseka ndi chonyozeka m'maso mwa anthu a mitundu yonse ya pa dziko lapansi. Kodi mwaiŵala zoipa zonse zimene adachita makolo anu, mafumu a ku Yuda ndi akazi ao, ndiponso inuyo ndi akazi anu, ku dziko la Yuda ndiponso pa miseu ya mu Yerusalemu? Mpaka lero lino simudalape, simudachite mantha, simudatsate malamulo anga amene ndidakuikirani inuyo ndi makolo anu. “Nchifukwa chake Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, Ndatsimikiza zoti ndiŵakhaulitse ndi kuŵatheratu anthu a ku Yuda. Ndidzatenga anthu otsala a ku Yuda amene adatsimikiza zopita ku Ejipito kukakhala kumeneko, onsewo adzatheratu. Adzaphedwa m'dziko la Ejipito, ena adzafa pa nkhondo, ena adzafa ndi njala. Ang'onoang'ono ndi akuluakulu omwe adzafadi pa nkhondo kapena kufa ndi njala. Ndipo adzasanduka chinthu chonyansa ndi chochititsa mantha, chinthu chomachiseka ndi chonyozeka. Ndidzalanga Ayuda okhala ku Ejipito monga momwe ndidalangira a ku Yerusalemu. Ndidzaŵalanga ndi nkhondo, njala ndi mliri. Motero mwa anthu otsala ku Yuda, amene adapita nakakhala ku Ejipito, palibe amene adzapulumuke, kapena kukhala moyo, kapena kubwerera ndi kukakhalanso ku Yuda komwe ankalakalaka. Palibe amene adzabwerere, kungopatula ena othaŵa nkhondo.” Tsono amuna onse amene adadziŵa kuti akazi ao ankafukizira lubani milungu ina, ndiponso akazi onse amene anali pamenepo, anthu ochuluka ndithu, kudzanso anthu onse amene ankakhala ku Patirosi m'dziko la Ejipito, adayankha Yeremiya kuti, “Ife sitidzamvera zimene watiwuza m'dzina la Chauta. Koma tidzachitadi zonse zimene tidalumbira. Tidzaifukizira ndithu lubani mfumukazi yakumwamba ndi kuiperekera nsembe zazakumwa, monga tinkachitira ifeyo ndi makolo athu, mafumu athu ndi akalonga athu, m'mizinda ya ku Yuda ndi m'miseu ya mu Yerusalemu. Nthaŵi imeneyo tinali ndi chakudya chambiri, ndipo tinkakhuta, osapeza zovuta. Koma kuchokera nthaŵi imene tidaleka kuifukizira lubani mfumukazi yakumwamba, ndi kumaiperekera nsembe zazakumwa, takhala tikusoŵa zonse, ndipo taonongeka ndi nkhondo ndi njala.” Akaziwo adapitirira ponena kuti, “Pamene tinkaifukizira lubani mfumukazi yakumwamba ndi kumaiperekera nsembe zazakumwa, kodi suja amuna athu ankavomereza m'mene tinkapangira mfumukaziyo makeke abwino olembapo chithunzi chake, ndiponso m'mene tinkaiperekera nsembe zazakumwa?” Atalimva yankho la anthu onsewo, amuna ndi akazi omwe, Yeremiya adati, “Za lubani amene munkafukiza inuyo, makolo anu, mafumu anu, akalonga anu ndi anthu am'dzikomo, m'mizinda ya ku Yuda ndi m'miseu ya mu Yerusalemu, kodi muyesa kuti Chauta adaziiŵala? Kodi nkupanda kuzikumbukira mumtima mwake? Nchifukwa chake Chauta sadathenso kupirira ntchito zanu zoipa ndi zonyansa zimene munkachita. Choncho dziko lanu lidasanduka chipululu, chinthu choopsa ndi chotembereredwa, dziko lopanda anthu, monga liliri leromu. Tsoka limeneli lakugwerani chifukwa choti munkafukiza lubani, ndipo munkachimwira Chauta pokana kumvera mau ake ndi posatsata malamulo ndi malangizo ake.” Yeremiya adauzanso anthu onse, makamaka akazi, kuti, “Mverani mau a Chauta inu nonse ochokera ku Yuda amene mukukhala ku Ejipito. Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akuti, Inu ndi akazi anu mudalonjeza ndi pakamwa panupa ndipo mudazichitadi ndi manja anu. Inu mudanena kuti, ‘Tidzachita zimene talumbira. Tidzaifukizira lubani mfumukazi yakumwamba ndi kuiperekera nsembe zazakumwa.’ Chabwino, tsimikizani lonjezo lanuli, ndi kuchitadi zimene mudalumbirazo. Koma tsono imvani mau a Chauta, inu nonse ochokera ku Yuda amene mumakhala ku Ejipito. Chauta akuti, Ndalumbira m'dzina langa lopambana kuti mwa anthu a ku Yuda palibe ndi mmodzi yemwe wodzatchulanso dzina limeneli m'dziko lino la Ejipito kuti, ‘Pali Chauta wamoyo.’ Panopo ndikuŵazonda kuti ndiŵachite zoipa osati zabwino. Anthu onse a ku Yuda amene ali ku Ejipito adzaphedwa pa nkhondo, ena adzafa ndi njala, mpaka nditaŵatheratu. Opulumuka ku nkhondo, amene adzabwerera ku Yuda kuchokera ku Ejipito, ndi oŵerengeka okha. Choncho otsala onse a ku Yuda amene adapita kukakhala ku Ejipito adzadziŵa kuti zoona nziti, zaozo kapena zangazi. Ndikukupatsani chizindikiro chakuti ndidzakulangani ku malo ano, kuti choncho mudziŵe kuti mau anga oti ndidzakulangani ndi oonadi. Chizindikirocho ndi ichi: Farao Hofira, mfumu ya ku Ejipito, ndidzampereka kwa adani ake, ndi kwa anthu ofuna kumupha, monga ndidamchitira Zedekiya mfumu ya ku Yuda: iyenso ndidampereka kwa mdani wake Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, amene ankafuna kumupha.” Naŵa mau amene mneneri Yeremiya adalembetsa Baruki mwana wa Neriya m'buku, chaka chachinai cha ufumu wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda: “Chauta, Mulungu wa Israele, akunena kuti, Iwe Baruki udati, ‘Tsoka kwa ine, poti Chauta wandiwonjezera chisoni pa mavuto anga onse. Ndatopa nako kubuula kwanga, sindikutha kupeza mpumulo konse!’ Chauta adandiwuza kuti ndilankhule mau aŵa kwa iwe Baruki, ‘Chimene ndidamanga, ndikuchigwetsa. Chimene ndidabzala, ndikuchizula. Umu ndi m'mene ndidzachitire ndi dziko lonse lapansi. Kodi ukudzifunira zazikulu? Ai, usadzifunire zoterezi. Ndidzagwetsera anthu onse zoipa. Koma iwe ndidzasunga moyo wako kulikonse kumene ungapite,’ ” akuterotu Chauta. Chauta adauza mneneri Yeremiya mau onena za anthu a mitundu ina. Kunena za Ejipito, adanena za gulu lankhondo la Farao Neko, mfumu ya ku Ejipito, limene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adaligonjetsa ku Karikemisi ku mtsinje wa Yufurate pa chaka chachinai cha ufumu wa Yehoyakimu, mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda. Adati, “Konzani zishango ndi malihawo, yambanipo wa ku nkhondo. Mangani akavalo, ndipo amene amakwerapo akwere. Khalani pa mzere mutavala zisoti zanu. Nolani mikondo yanu, valani malaya anu achitsulo. Koma tsopano ndikuwona chiyani? Achita mantha, abwerera. Ankhondo ao agonjetsedwa. Akuthaŵa kaŵeraŵera, osacheukanso m'mbuyo. Agwidwa ndi mantha ponseponse,” akutero Chauta. Waliŵiro sangathe kupulumuka. Ngakhale wankhondo wamphamvu sangathe kudzipulumutsa. Akunka naphunthwa, kumagwa kumpoto kwa mtsinje wa Yufurate. “Kodi ndani akukwera ngati mtsinje wa Nailo, ngati mitsinje ya madzi achigumula? Ejipito akukwera ngati mtsinje wa Nailo, ngati mitsinje ya madzi achigumula. Akuti, ‘Ndidzambatuka ndi kuliphimba dziko lapansi. Ndiwononga mizinda ndi anthu ake.’ Tiyeni inu akavalo, thamangani inu magaleta. Pitani patsogolo inu ankhondo, inu anthu a ku Etiopiya ndi a ku Puti, ogwira zishango, ndiponso inu anthu a ku Ludi, akatswiri pogwira uta. Koma tsikulo ndi tsiku la Chauta Wamphamvuzonse, tsiku lolipsira, lolipsira adani ake. Lupanga lake lidzaŵaononga, lidzakhuta magazi, lidzachita kuledzera nawo. Ambuye Chauta Wamphamvuzonse akukonzera nsembe ku dziko lakumpoto, pafupi ndi mtsinje wa Yufurate. Pita ku Giliyadi, ukatenge mankhwala, namwali iwe Ejipito. Wayesayesa mankhwala ambiri koma walephera, matenda akowo sadzachira. Anthu a mitundu ina amva za manyazi ako, kulira kwako kwadzaza dziko lapansi. Ankhondo akunka nagwetsanagwetsana, onse pansi ndu kugwera limodzi.” Naŵa mau amene Chauta adalankhula ndi mneneri Yeremiya za kubwera kwa Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, kudzathira nkhondo dziko la Ejipito: “Mulengeze ku Ejipito, mulalike ku Migidoli, ku Memfisi ndi ku Tapanesi. Anthu akumeneko muŵauze kuti, ‘Imani pamalo panu, mukhale okonzeka chifukwa chakuti nkhondo idzaononga zonse pokuzungulirani.’ Chifukwa chiyani mulungu wanu Apisi wathaŵa? Chifukwa chiyani nkhunzi yanu yoipembedza ija sidalimbike? Nchifukwa choti Chauta waigwetsa. Anthu ako akukhumudwa, akugwerana. Aliyense akunena kuti, ‘Nyamukani, tiyeni tizibwerera kwathu, kudziko kumene tidabadwira, tithaŵe lupanga la adani athuŵa!’ Farao, mfumu ya ku Ejipito, mpatseni dzina lakuti ‘Waphokoso, wotaya mwai wake.’ “Pali Ine ndemwe!” Ikutero Mfumu, imene dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse. Wina wamphamvu adzabwera wonga ngati Tabori phiri lopambana mapiri ena, wonga ngati phiri la Karimele, loti joo m'mbali mwa nyanja. Konzani katundu wanu wopita naye ku ukapolo, inu anthu a ku Ejipito, pakuti Memfisi adzasanduka chipululu, ngati bwinja, mopanda anthu. “Ejipito ali ngati mwanawang'ombe wokongola. Koma chimphanga chochokera kumpoto chidzamtera. Ankhondo aganyu amene ali nawo, ali ngati anaang'ombe onenepa. Nawonso abwerera m'mbuyo nathaŵa pamodzi, palibe amene walimbikira. Ndithu, nthaŵi ya tsoka yaŵafikira, ndiyo nthaŵi yoŵalanga! “Liwu la Ejipito likunga ngati la njoka yothaŵa, chifukwa choti adani ake abwera ndi zida zao, kubwera ndi nkhwangwa, ngati anthu odula mitengo. Adzaduladi nkhalango ya ku Ejipito ngakhale njoŵirira, chifukwa anthuwo ndi ochuluka ngati dzombe, sangathe kuŵerengeka. Anthu a ku Ejipito adzachitadi manyazi, adzatengedwa ukapolo ndi anthu akumpoto,” akutero Chauta. Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, wanena kuti, “Ndidzalanga Amoni, mulungu wa Thebesi. Ndidzalanganso Farao ndi Ejipito pamodzi ndi milungu yake ndi akalonga ake. Ndidzalanga Farao ndi onse amene amamkhulupirira. Ndidzaŵapereka kwa amene afuna kuŵaononga, ndiye kuti kwa Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, ndi atsogoleri ake a ankhondo. Komabe patapita nthaŵi, Ejipito adzakhalanso ndi anthu monga kale,” akutero Chauta. “Koma iwe Yakobe, mtumiki wanga, usachite mantha, Iwe Israele, usataye mtima, chifukwa ndidzakupulumutsa kuchokera ku maiko akutali. Ndidzapulumutsanso zidzukulu zako kuchokera kumaiko kumene adapita nazo ku ukapolo. Yakobe adzabwerera, nadzapumula pabwino, ndi pa mtendere. Palibe winanso amene adzamuwopsa.” Chauta akunena kuti, “Iwe Yakobe, mtumiki wanga, usachite mantha, pakuti Ine ndili nawe. Ndidzaonongeratu mitundu yonse ya anthu a kumaiko kumene ndidakupirikitsira. Koma iweyo sindidzakuwononga kotheratu ai. Kulanga ndidzakulanga monga m'mene kuyenera, sindingakulekelere osakulanga konse.” Naŵa mau amene Chauta adalankhula ndi mneneri Yeremiya, onena za Afilisti, Farao asanaononge Gaza. Adati, “Onani m'mene madzi akubwerera kuchokera kumpoto, adzakhala mtsinje wosefukira ndi wamkokomo. Adzasefukira m'dzikomo ndi kumiza zonse zokhala m'menemo, mizinda yonse, ndi anthu onse okhalamo. Anthu azidzafuula, onse okhala m'dzikomo azidzalira. Adzamva mgugu wa akavalo othamanga, adzamva phokoso la magaleta ake, ndi kulira kwa mikombero yake. Atate sadzaganizirako za ana ao, adzangokhala ali manja lende! Ndithu tsiku lidzafika limene Afilisti onse adzaonongeka, tsiku limene adzaphedwe otsala onse amene ati adzathandize mzinda wa Tiro ndi Sidoni. Pakuti Chauta adzaononga Afilisti, onse otsala a ku chilumba cha Krete. A ku Gaza adzameta mipala yachisoni, A ku Asikeloni adzangoti chete. Inu otsala mwa Afilisti, kodi ndi mpaka liti mudzakhale mukudzichekacheka chifukwa cha kulira? Mukuti, ‘Ha, Chauta lupanga lili m'manja! Kodi adzapumula liti? Aliloŵetse m'chimake, likhale momwemo, lipumule.’ Kodi lupangalo lingapumule bwanji pamene Chauta walipatsa kale ntchito yoti limchitire? Walituma kuti likalimbane ndi Asikeloni, kuti likathire nkhondo anthu a m'mbali mwa nyanja.” Ponena za Mowabu, Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akuti, “Tsoka kwa mzinda wa Nebo, wasanduka chipululu. Kiriyataimu wachititsidwa manyazi, wagonjetsedwa. Linga lake lankhondo alinyoza ndipo aligumula. Mowabu sakutchukanso. Adampanganirana zachiwembu ku Hesiboni, adati, ‘Tiyeni timuwononge, asakhalenso mtundu wa anthu.’ Ndipo inu okhala ku Madimeni, adzakukhalitsani chete, adzakupirikitsani ndi lupanga. “Imvani kulira kwachisoni kwa anthu a ku Horonaimu, akuti, ‘Chisakazo ndi chiwonongeko chachikulutu!’ Mowabu waonongeka, ana ake akulira kwambiri. Anthu akupita nalira kwambiri pa chikwera cha ku Luhiti. Kulira kwa chiwonongeko kukumveka ku matsitso a ku Horonaimu. Thaŵani, mudzipulumutse. Thamangani ngati mbidzi yam'chipululu. Inunso mudzagwidwa chifukwa choti munkadalira ntchito zanu ndi chuma chanu. Kemosi, mulungu wanu, adzatengedwa ukapolo, pamodzi ndi ansembe ake ndi akalonga ake. Woononga uja adzasakaza mzinda uliwonse, palibe mzinda ndi umodzi womwe umene udzapulumuke. Malo am'zigwa adzaonongeka, malo okwera nawonso adzasakazika. Zidzachitika monga momwe Chauta adanenera. “Mowabu mchenjezeni, chifukwa posachedwa asakazika. Mizinda yake isanduka mabwinja, ikhala yopanda anthu. “Ndi wotembereredwa amene amagwira ntchito ya Chauta mwaulesi. Ndi wotembereredwa amene amaletsa lupanga lake kutema ndi kupha anthu. Mowabu wakhala pa mtendere kuyambira unyamata wake, ngati vinyo wokhazikika pa masese ake, osapungulidwa kuchoka mu mtsuko wina kuthira mu mtsuko wina. Sadatengedwe ukapolo. Nchifukwa chake khalidwe lake lili losasinthika, ndipo fungo lake lili lomwe lija.” Chauta akunena kuti, “Chenjerani tsono, akubwera masiku pamene ndidzatuma anthu oti Mowabuyo adzamkhuthule ngati vinyo. Kenaka mitsuko yake itasanduka yopanda kanthu m'kati, ndidzaiphwanya. Motero Mowabu adzachita manyazi ndi Kemosi, mulungu wake, monga momwe Israele adachitira naye manyazi Betele, mulungu amene ankamukhulupirira. “Kodi mungathe kunena bwanji kuti, ‘Ife ndife ngwazi, asilikali olimba mtima pa nkhondo?’ Woononga Mowabu ndi mizinda yake wabwera. Anyamata ake asee akupita kukaphedwa. Ikutero mfumu imene dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse. Kugwa kwa Mowabu kuli pafupi. Chiwonongeko changokhala pang'onong'ono kuti chimugwere. Mumvereni chisoni kwambiri inu nonse anansi ake, anzake nonse amene mumamdziŵa. Ndipo munene kuti, ‘Ogo, taonani m'mene yathyokera ndodo yachifumu yamphamvu ija! Taonani m'mene yathyokera ndodo yaulemu ija!’ “Inu anthu a ku Diboni, tsikanipo pa ulemerero wanu, khalani pansi poumapa. Woononga Mowabu wafika kudzamenyana nanu, wapasula malinga anu ankhondo. Inu amene mumakhala ku Aroere, imani m'mbali mwa mseu muziwonerera. Mufunse mwamuna amene wathaŵa ndiponso mkazi amene wapulumuka, munene kuti, ‘Kodi kwagwanji?’ Iwo adzayankha kuti, ‘Ukutu Mowabu wagwa, amchititsa manyazi, mlireni mofuula. Mulengeze ku mtsinje wa Arinoni kuti Mowabu wasanduka bwinja.’ “Chiweruzo chafika ku dziko lakumapiri, ndiye kuti mizinda iyi: Holoni, Yaza, Mefati ndi Diboni, Nebo ndi Betedibilataimu, Kiriyataimu, Betegamuli, Betemeoni, Keriyoti, Bozira ndi mizinda yonse ya ku Mowabu, yakutali ndi yakufupi. Mphamvu za Mowabu zaonongeka, mkono wake wolimba wathyoka,” akutero Chauta. “Mledzeretseni Mowabu chifukwa adadzikuza poukira Chauta. Avimvinizike m'masanzi ake omwe. Akhale chinthu chomachiseka. Kodi suja Israele adaali chinthu chonyozeka kwa iwe? Kodi adapezeka pakati pa mbala, kuti nthaŵi zonse polankhula za iye uzimpukusira mutu momunyoza?” Chauta akuti, “Inu okhala ku Mowabu, siyani mizinda yanu. Kapezeni pokhala pakati pa mathanthwe. Mukhale ngati nkhunda yomanga chisa kukamwa kwa phanga. Tamva za kunyada kwa Mowabu, ndi wonyadadi kwabasi. Ndi wodzikweza, wodzitama, wodzitukumula, ndipo ndi wa mtima wodzimva zedi. Ndikudziŵa kudzikuza kwake. Mau ake odzitama ngachabechabe, ntchito zake nzopanda pake. Motero ndikulira chifukwa cha Mowabu. Ndikulira mwachisoni chifukwa cha anthu onse a ku Mowabu. Ndikulira anthu a ku Kiriheresi. Ndikulira anthu a ku Sibima kupambana m'mene ndidalirira anthu a ku Yazere. Iwe mzinda wa Sibima, uli ngati mpesa umene nthambi zake zidatambalala mpaka ku nyanja, kukafika mpaka ku Yazere. Woononga wasakaza zipatso zako zam'chilimwe, wasakaza mipesa yako yonse. Kusangalala ndi kukondwa kwa dziko lachonde la Mowabu kwatha. Ndaletsa kuchucha kwa vinyo mopondera mphesa. Palibe amene akufuula mokondwa akamaponda mphesa. Kufuula kulipo, koma si kufuula kokondwa ai. “A ku Hesiboni ndi a ku Eleale akulira movutika. Kulira kwao kukumveka mpaka ku Yaza, kuchokera ku Zowari mpaka ku Horonaimu ndi ku Egilati-Selisiya. Ngakhale madzi a ku Nimurimu aphwa. Ndidzaŵaphadi Amowabu amene amapereka nsembe ku akachisi ku mapiri, ndi kufukiza lubani kwa milungu yao,” akutero Chauta. “Nchifukwa chake mtima wanga ukulira Mowabu ngati chitoliro. Mtima wanga ukulira anthu a ku Kiriheresi ngati chitoliro, chifukwa chuma chao chonse chimene adaachipata chatheratu. Kumutu kwa munthu aliyense nkometa, ndevu nazonso nzometa, manja onse ndi ochekekachekeka, ndipo m'chiwuno mwao avala ziguduli. Pa madenga onse a ku Mowabu ndiponso m'miseu yake simukumvekanso kanthu kena, koma kulira kokha. Ndamtswanya Mowabu ngati chiŵiya chopanda ntchito. Taonani m'mene watswanyikira! Tamvani m'mene akulirira anthu ake! Taonani m'mene wakhalira chofulatira mwamanyazi! Mowabu wasanduka chinthu chonyozeka, chinthu chochititsa mantha kwa anzake okhala nawo pafupi,” akutero Chauta. Chauta akunena kuti, “Mtundu wina udzachita kuuluka nkudzagwera Mowabu ngati nkhwazi ya mapiko otambalitsa. Mizinda idzagwidwa, malinga adzalandidwa. Tsiku limenelo mitima ya ankhondo a ku Mowabu idzakhala ili thithithi ndi mantha, ngati mkazi pa nthaŵi yake yochira. Mowabu adzaonongeka, sadzakhalanso mtundu wa anthu, pakuti adadzikuza poukira Chauta. Nkhaŵa, dzenje ndi msampha zikuyembekeza inu anthu okhala ku Mowabu,” akutero Chauta. “Wothaŵa nkhaŵa, adzagwa m'dzenje. Wotuluka m'dzenje, adzakodwa mu msampha. Zimenezi nzimene ndidzamgwetsere Mowabu pa nthaŵi ya chilango chake,” akutero Chauta. “Amene akuthaŵa, amaima pa mthunzi wa Hesiboni, chifukwa chotopa kwambiri. Koma moto wayaka kuchokera ku Hesiboni, malaŵi a moto abuka kuchokera ku nyumba ya mfumu Sihoni, ndipo motowo ukuwononga mapiri a ku Mowabu, dziko la anthu andeu. Tsoka kwa iwe Mowabu! Anthu opembedza Kemosi atha. Ana ako onse aamuna ndi aakazi adatengedwa ukapolo. Komabe masiku akutsogolo ndidzambwezeranso ufulu Mowabu,” akutero Chauta. Chiweruzo cha Mowabu chathera pamenepa. Za Aamoni, Chauta akufunsa kuti, “Kodi Israele alibe ana aamuna? Kodi alibe mloŵachuma? Chifukwa chiyani tsono anthu opembedza Milikomu alanda dziko la Gadi, ndipo akukhala m'mizinda yake? Ndipotu nthaŵi ikudza, pamene ndidzamveketse mfuu wankhondo ku Raba, likulu la ku Amoni. Mzinda umenewo udzasanduka bwinja lopanda anthu, ndipo midzi yake idzapserera. Tsono Israele adzaŵalanda zao adaniwo amene adamulanda zake,” akutero Chauta. “Lirani, inu a ku Hesiboni, pakuti mzinda wa Ai waonongeka. Lirani chokweza, inu ana aakazi a ku Raba. Valani ziguduli kuwonetsa chisoni, mulire, muthaŵire uku ndi uku m'kati mwa machinga. Ndithu, mulungu wanu Milikomu adzatengedwa ukapolo, pamodzi ndi ansembe ake ndi akalonga ake. Chifukwa chiyani mukunyadira zigwa zanu, inu anthu osakhulupirika, amene munkadalira chuma chanu nkumati, ‘Ndani angalimbane ndi ife?’ ” Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Chenjerani, mudzaona zoopsa kuchokera kwa onse okuzungulirani. Adzakupirikitsani muli kaŵeraŵera, popanda wina wokusonkhanitsaninso othaŵanu. Komabe pambuyo pake ndidzaŵabwezera ufulu Aamoni,” akutero Chauta. Za Edomu, Chauta Wamphamvuzonse akufunsa kuti, “Kodi nzeru sizikupezekanso ku Tema? Kodi anzeru uphungu wao udatheratu? Kodi nzeru zao zija zati zii? Anthu a ku Dedani bwererani, thaŵani mukakhale ku makwaŵa. Ndithudi ndidzalanga zidzukulu za Esau pa tsiku lake la chiweruzo. Othyola mphesa akadakwera kwa inu, akadakusiyiraniko mphesa pa nthambi. Mbala zikadafika usiku, bwenzi zitangotengako zofunikira zokha. Koma ine ndachotseratu chuma chonse cha zidzukulu za Esau. Ndaonetsa poyera malo ao obisalamo, alibenso poti angabisale. Ana ao, abale ao ndi anansi ao omwe aonongeka. Palibe wina amene watsalako. Siyani ana anu amasiye, ndidzaŵalera ndine. Akazi anu amasiye akhoza kudalira Ine.” Chauta akunena kuti, “Ngati amene sanali oyenera kumwa chikho cha chilango adzamwe ndithu, nanji inu, muyesa mudzakhala osalangidwa? Pepani, mudzalangidwa ndithu, ndipo mudzamwadi chikhocho. Pali Ine ndemwe, mzinda wa Bozira udzasanduka chinthu chochititsa nyansi, chomachiseka, chopanda kanthu ndi chotembereredwa. Ndipo midzi yake yonse idzakhala mabwinja mpaka muyaya.” Ndamva uthenga wochokera kwa Chauta wamthenga watumidwa kwa anthu a mitundu ina. Akufuula kuti, “Sonkhanani pamodzi kuti mumenyane ndi Edomu, dzambatukani mukonzekere nkhondo! Ndidzakuchepetsa pakati pa mitundu yonse, anthu onse adzakunyoza. Kunyada kwako kwakunyenga, kuwopseza kwako kwakusokeza, iwe wokhala m'mapanga ndi m'matanthwe, ku mapiri. Ngakhale umange chisa chako pamwambamwamba ngati nkhwazi, ndidzakutsitsabe pamenepo,” akutero Chauta. “Dziko la Edomu lidzasanduka lochititsa nyansi. Onse odutsamo azidzachita nyansi, nkumatsonya chifukwa cha kuwonongeka kwake koopsa. Monga momwe udaonongekera mzinda wa Sodomu ndi wa Gomora pamodzi ndi midzi yake yozungulira, momwemonso sikudzakhalako munthu ndi mmodzi yemwe kumeneko. Palibe ndi mmodzi yemwe wodzayendako kumeneko. Monga momwe mkango wotuluka ku nkhalango za ku Yordani umaopsera khola la nkhosa lotetezedwa bwino, Inenso mwadzidzidzi ndidzapirikitsira Aedomu kutali ndi kwao. Pambuyo pake ndidzaŵaikira woŵalamulira amene ndidzamufune Ine. Nanga ndani angafanefane ndi Ine? Ndani angandipititse kubwalo lamilandu? Ndi mtsogoleri uti amene angalimbike pamaso panga? Nchifukwa chake imvani, zimene Ine Chauta ndakonza zolangira Edomu, ndiponso zolinga zake zolangira anthu a ku Temani ndi izi: Ana ao omwe adzatengedwa ndithu, ndipo anthu onse adzada nalo nkhaŵa tsoka lao. Dziko lapansi lidzanjenjemera chifukwa cha kugwa kwao. Kulira kwao kudzamveka mpaka ku Nyanja Yofiira. Ndithu mtundu wina udzachita kuuluka nkudzagwera Bozira ngati nkhwazi ya mapiko otambalitsa. Pa tsiku limenelo mitima ya ankhondo a ku Edomu idzakhala ili thithithi ndi mantha, ngati mkazi pa nthaŵi yake yochira.” Za Damasiko Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Anthu a ku Hamati ndi ku Aripadi asokonezeka, chifukwa adamva uthenga woipa. Mtima wao wachita kuti phwi ndi mantha, ndi osakhazikika ngati nyanja yosatha kukhala bata. Damasiko wataya mtima, akufuna kuthaŵa chifukwa chogwidwa ndi mantha aakulu. Akumva nkhaŵa ndi zoŵaŵa zonga za mkazi pa nthaŵi yake yochira. Mzinda wotchuka uja wasiyidwa, mzinda wachikondwerero uja! Nchifukwa chake anyamata ake adzagwa m'mabwalo ake, ndipo ankhondo ake onse adzaonongedwa tsiku limenelo. Ndidzatentha malinga a Damasiko, moto wake udzapsereza nyumba zamphamvu za Benihadadi.” Kunena za Kedara ndi za maufumu a ku Hazori amene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adagonjetsa, Chauta akunena kuti, “Nyamukani mukaŵathire nkhondo ku Kedara! Aonongeni anthu akuvumawo! Gwetsani mahema ao ndipo mulande nkhosa zao. Tengani nsalu ndi katundu wao yense m'mahemamo. Landaninso ngamira zao. Anthu adzafuula kwa iwo kuti, ‘Pali zoopsa pa mbali zonsezonse!’ Inu anthu a ku Hazori, thaŵani, fulumirani, kabisaleni ku makwaŵa. Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, wakonzekera kuti amenyane nanu,” akutero Chauta. “Nyamukani, kauthireni nkhondo mtundu wa anthuwo umene uli pa mtendere, anthu amene akuyesa kuti ali pabwino. Mzinda wao ndi wopanda zipata kapena mipiringidzo, udangokhala pawokha. Ngamira zao zidzafunkhidwa, ndipo makola ao a ng'ombe adzalandidwa. Ndidzaŵabalalitsira ku mphepo zonse zinai onse ometa tsitsi lao cham'mbali. Ndidzaŵagwetsera zoopsa kuchokera ku mbali zonse. Hazori adzasanduka bwinja, malo a nkhandwe, mpaka muyaya. Simudzakhalanso munthu m'menemo,” akutero Chauta. Zedekiya, mfumu ya ku Yuda, atangoyamba kumene kulamulira, Chauta adalankhula ndi mneneri Yeremiya za Elamu. Adati, “Tamvera, ndidzathyola uta wa Elamu umene ndiye chida chake champhamvu. Ndidzafitsa mphepo zinai pa anthu a ku Elamu kuchokera ku mbali zonse za mlengalenga. Ndidzaŵamwazira ku mphepo zinaizo ndipo silidzakhalapo dziko kumene anthuwo sadzafikako. A ku Elamuwo ndidzaŵachititsa mantha pamaso pa adani ao ndiponso pamaso pa amene afuna kuwononga moyo wao. Ndidzaŵagwetsera mkwiyo wanga waukali. Ndidzaŵapirikitsa ndi lupanga mpaka kuŵatheratu. Tsono ndidzaika mpando wanga waufumu ku Elamu. Kumeneko ndidzaononga mfumu ndi akalonga ake. Komabe, patsogolo pake ndidzaŵabwezera ufulu anthu a ku Elamu,” akutero Chauta. Naŵa mau amene Chauta adalankhula ndi mneneri Yeremiya kunena za mzinda wa Babiloni ndi anthu ake. Adati, “Ulengeze ndi kulalika kwa anthu a mitundu yonse. Kweza mbendera ndipo usabise kanthu, uŵauze kuti, ‘Babiloni wagwa! Mulungu wake Beli wachititsidwa manyazi, nayenso Merodaki wataya mtima. Mafano ake anyozedwa kwambiri, milungu yake yataya mtima.’ “Mtundu wa anthu akumpoto wadzauthira nkhondo mzinda wa Babiloni. Dziko lake adzalisandutsa bwinja, ndipo kumeneko sikudzakhalanso munthu kapena nyama.” Chauta akunena kuti, “Masiku amenewo, nthaŵi imeneyo Aisraele ndi Ayuda adzasonkhana pamodzi, azikabwera nalira. Adzafunitsitsa kuchita zimene Chauta Mulungu wao afuna. Adzafunsa njira ya ku Ziyoni, nkuyamba ulendo wobwerera kumeneko. Adzati, ‘Tiyeni tibwerere kwa Chauta, tikachite naye chipangano chamuyaya, chimene sichidzaiŵalika konse.’ “Anthu anga anali ngati nkhosa zotayika. Abusa ao adaŵasokeza ndi kuŵayalukitsa ku mapiri. Ankangoyendayenda ku zitunda ndi ku mapiri, mpaka kuiŵala kwao. Aliyense amene adaŵapeza, adaŵaononga. Ndipo adani ao ankati, ‘Ifetu tilibe mlandu, chifukwa choti iwoŵa adachimwira Chauta amene ndiye pokhala pao penipeni, amenenso makolo ao ankamkhulupirira.’ “Thaŵaniko ku Babiloni. Chokaniko ku dziko la Ababiloni, muyambe ndinu kutuluka, ngati atonde otsogolera ziŵeto. Ndidzasankha ndi kubwera nalo gulu lankhondo lamphamvu la mitundu ina ya anthu lochokera kumpoto, kuti lidzamenyane ndi Babiloni. Mivi yao ili ngati ya wankhondo waluso, yosapita padera. Ababiloni adzafunkhidwa, ndipo onse oŵafunkha adzakhuta,” akutero Chauta. “Inu Ababiloni, mudaononga anthu anga osankhidwa. Ngakhale mukondwe ndi kusangalala, ngakhale mulumphelumphe mokondwa ngati mwanawang'ombe wopuntha tirigu, ngakhale mulire monyada ngati akavalo, mzinda wanu udzachititsidwa manyazi ndithu kwambiri. Mzinda umene uli ngati mai wanu adzaunyazitsa. Ndithudi, Ababiloni adzakhala otsirizira mwa anthu a mitundu yonse. Mzinda wao udzakhala ngati thengo, ngati dziko louma lachipululu. Udzakhala wopanda anthu chifukwa cha mkwiyo wa Chauta, udzakhala chipululu chokhachokha. Onse odutsa ku Babiloni azidzachita nyansi, nkumangotsonya chifukwa cha mabala a mzindawo. Konzekani kuti mumzinge Babiloni pa mbali zonse, inu okoka mauta. Mlaseni, chulukitsani mivi yanu. Iye uja adachimwira Chauta. Mfuulireni ponseponse pakuti wagonja. Nsanja zake zagwa, malinga ake aonongeka. Kumeneku ndiko kulipsira kwa Chauta. Mlipsireni, mumchite zonga zomwe iye adaŵachita ena. Ku Babiloniko chotsani wofesa aliyense ndiponso aliyense wodula tirigu ndi chikwakwa chake pa nthaŵi yokolola. Poopa lupanga la ozunza anzao, aliyense adzatembenukira kwa anthu ake, nkuthaŵira ku dziko lakwao.” Aisraele ali ngati nkhosa zomwazika, zopirikitsidwa ndi mikango. Mfumu ya ku Asiriya ndiyo idayamba kuŵapha Aisraelewo, nkudzabwera Nebukadinezara mfumu wa ku Babiloni kudzachita ngati kupwepweta mafupa ao. Nchifukwa chake Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, “Ndidzailanga mfumu ya ku Babiloniyo pamodzi ndi dziko lake, monga momwe ndidalangira mfumu ya ku Asiriya. Israele ndidzambwezera kubusa kwake, ndipo azikadya ku Karimele ndi ku Basani. Adzadya chakudya chokwanira ku mapiri a ku Efuremu ndi ku Giliyadi. Pa masiku amenewo, nthaŵi imeneyi ikadzafika, adzafunafuna zolakwa za Israele, koma sichidzapezeka nchimodzi chomwe. Adzafufuzafufuza machimo a Yuda, koma silidzapezeka nlimodzi lomwe. Pakuti otsala amene ndaŵasiya aja ndidzaŵakhululukira,” akutero Chauta. “Lithireni nkhondo dziko la Merataimu ndi anthu okhala ku Pekodi. Muŵaphe ndi lupanga ndi kuŵaonongeratu. Muchite zonse zimene ndakulamulani,” akutero Chauta. “Phokoso la nkhondo likumveka m'dziko, ndiponso pali chiwonongeko chachikulu. Amene anali ngati nyundo ya dziko lapansi uja, onani m'mene aphwanyikira. Onani m'mene Babiloni wasandukira chinthu chonyansa pakati pa mitundu ya anthu. Iwe Babiloni, ndakutchera msampha ndipo wakodwamo, iwe osazindikira kanthu. Udapezeka ndipo udagwidwa chifukwa chakuti udaalimbana ndi Chauta. Chauta watsekula nyumba ya zida zake, ndipo watulutsa zida za mkwiyo wake. Paja Chauta Wamphamvuzonse ali ndi ntchito yoti agwire ku dziko la Ababiloni. Mumenyane naye Babiloni mbali zonsezonse. Tsekulani nkhokwe zake. Anthu ake muŵaunjike ngati milu ya tirigu, ndipo muŵaononge kotheratu, pasakhale wopulumuka ndi mmodzi yemwe. Iphani anyamata ake onse ankhondo. Onse aphedwe ndithu. Tsoka laŵagwera pakuti tsiku lao la chilango lafika.” “Ndikumva anthu othaŵa nkhondo ya ku Babiloni akulengeza za kulipsira kwa Chauta, Mulungu wathu, kulipsirira chifukwa choononga Nyumba yake.” “Muitane onse oponya mivi kuti amthire nkhondo Babiloni, abwerenso onse okoka mauta. Mzingeni ndi zithando zankhondo kuti asathaŵepo munthu ndi mmodzi yemwe. Mlangeni potsata zolakwa zake. Mchiteni zomwe iye adaŵachita ena. Iyeyu adanyoza Chauta, Woyera uja wa Israele. Nchifukwa chake anyamata ake adzagwa m'mabwalo ake. Ndipo ankhondo ake onse adzaonongeka tsiku limenelo,” akutero Chauta. “Ndikukuthira nkhondo, mzinda wachipongwewe, pakuti yakwana nthaŵi yako, lafika tsiku lako la chilango,” akutero Chauta Wamphamvuzonse. “Mtundu wodzikuzawe, udzaphunthwa nkugwa, ndipo palibe amene adzakudzutse. Mizinda yako ndidzaitentha ndi moto, motowo udzapsereza zonse zoyandikana nayo mizindayo.” Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Anthu a ku Israele akuzunzidwa pamodzi ndi anthu a ku Yuda. Onse amene adaŵagwira ukapolo aŵagwiritsa, osafuna kuŵamasula. Koma mpulumutsi wao ndi wamphamvu, dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse. Adzaŵaimira pa mlandu, kuti apatse mtendere dziko lonse lapansi, koma adzavutitsa okhala ku Babiloni. “Lupanga lankhondo lilunjika pa Ababiloni, Imfa iloze pa anthu a ku Babiloni, pa akuluakulu ao ndi pa anthu ao anzeru,” akutero Chauta. “Lupanga lilunjike pa anthu oombeza, kuti asanduke zitsilu. Lilunjikenso pa ankhondo ake, kuti aonongedwe. Lupanga lilunjike pa akavalo ake ndi pa magaleta ake, lilunjikenso pa magulu ankhondo achilendo amene ali pakati pao, kuti asanduke ngati akazi. Lupanga lilunjike pa chuma chake chonse, kuti chidzafunkhidwe. Chilala chilunjike pa madzi ake, kuti adzaphwe. Paja dzikolo nlamafano, anthu ake achita kuyaluka nawo mafanowo. “Nchifukwa chake ku Babiloni nyama zakuthengo zizidzakhalira limodzi ndi afisi, ndipo nthiŵatiŵa zizidzakhalamonso. Tsono kumeneko sikudzakhala anthu mpaka muyaya. Sikudzapezeka munthu ndi mmodzi yemwe pa mibadwo yonse. Monga momwe Mulungu adaonongera Sodomu ndi Gomora ndi mizinda yonse yozungulira, momwemonso palibe munthu amene adzakhale kumeneko. Palibe ndi mmodzi yemwe amene azidzayendako. “Onani, ankhondo akubwera kuchokera kumpoto. Anthu a mtundu wanyonga ndi mafumu ambiri akunyamuka kuchokera ku madera akutali a dziko lonse lapansi. Atenga mauta ndi mikondo, ngankhalwetu, ndiponso opanda chifundo. Phokoso lao lili ngati mkokomo wa nyanja. Akwera pa akavalo, atavala zankhondo, kuti adzamenyane nawe, iwe mzinda wa Babiloni. Mfumu ya ku Babiloni idamva za mbiri yao, ndipo yachita kuti m'nkhongono zii! Yada nkhaŵa, ikumva kuŵaŵa ngati mkazi pa nthaŵi yake yochira. “Monga momwe mkango wotuluka ku nkhalango za ku Yordani umaopsera khola lankhosa lotetezedwa bwino, Inenso mwadzidzidzi ndidzapirikitsira Ababiloni kutali ndi kwao. Pambuyo pake ndidzaŵaikira woŵalamulira amene ndidzamufune Ine. Nanga ndani angafanefane ndi Ine? Ndani angandipititse ku bwalo lamilandu? Ndi mtsogoleri uti amene angalimbike pamaso panga? Nchifukwa chake imvani, zimene Ine Chauta ndakonza zolangira Babiloni, ndiponso zolinga zanga zolangira dziko la Ababiloni ndi izi: Ndithudi, ndi ana omwe adzatengedwa, ndipo onse adzada nalo nkhaŵa tsoka lao. Dziko lonse lapansi lidzanjenjemera chifukwa cha kugwa kwa Babiloni. Kulira kwake kudzamveka pakati pa mitundu yonse ya anthu.” Chauta akunena kuti, “Ndidzautsa mphepo yoti idzaononge Babiloni pamodzi ndi onse okhala m'dziko la Babiloni. Ndidzatuma alendo ku Babiloni, kuti adzampepete ndi kuseseratu zonse zokhala m'dziko lake. Iwowo adzamuukira pa mbali zonse nthaŵi ya zoopsayo. Okoka uta musaŵalekerere, kapena onyadira chovala chao chankhondo. Anyamata ake musasiyeko ndi mmodzi yemwe. Ankhondo ake onse muŵaononge. Adzavulazidwa ndi kufera m'dziko lonse ndi m'miseu ya mzinda wao womwe. Israele ndi Yuda sadasiyidwe ndi Mulungu wao, Chauta Wamphamvuzonse. Koma dziko la Ababiloni nlodzaza ndi machimo, machimo ake onyoza Woyera uja wa Israele. “Aliyense mwa inu athaŵe, achoke ku Babiloni kuti apulumutse moyo wake. Musaphedwe naye pamodzi pamene adzalandira chilango chake. Limeneli ndilodi tsiku limene Chauta adzaŵalanga, ndipo adzaŵalipsira kwathunthu. Pajatu Babiloni anali ngati chikho chagolide m'manja mwa Chauta, kuti aledzeretse dziko lonse lapansi. Mitundu yambiri ya anthu idamwako vinyo wake, nchifukwa chake idapenga. Babiloni wagwa mwadzidzidzi ndipo waonongeka. Mlireni, mfunireni mankhwala, kuti mwina nkuchira. Ena adati, ‘Tidayesa kumpatsa mankhwala koma sadachire. Tiyeni tingomsiya, timchokere ndipo aliyense apite ku dziko lakwao. Paja mlandu wake wafika mpaka kumwamba, wafika mpaka ku mlengalenga.’ ” Tsono Chauta waonetsa poyera kuti ifeyo ndife osalakwa. Tiyeni tilengeze ku Ziyoni zimene Chauta, Mulungu wathu, watichitira. “Songolani mivi, tengani zishango.” Chauta wautsa mitima ya mafumu a Amedi, poti cholinga chake nchoti aononge Babiloni. Afuna kumlipsira chifukwa choononga Nyumba yake. Kwezani mbendera yankhondo ndipo muwononge malinga a Babiloni. Mulimbitse oteteza, muike alonda, mukonzekere kulalira. Pakuti Chauta watsimikiza, ndipo adzachitadi zimene adanena za anthu a ku Babiloni. Inu amene muli ndi mitsinje yambiri, ndinu olemera kwambiri, koma chimalizo chanu chafika, moyo wanu watha. Chauta Wamphamvuzonse adalumbira pali Iye yemwe mwini wake kuti, “Ndidzatuma anthu osaŵerengeka ngati dzombe kuti adzakuthireni nkhondo, ndipo adzafuula, kuwonetsa kuti apambana.” Chauta ndiye amene adalenga dziko lapansi ndi mphamvu zake. Ndiye amene adapanga zonse ndi nzeru zake, ndipo ndi umisiri wake adayala thambo lakumwamba. Iye akalankhula, kumamveka mkokomo wa madzi kumwamba, ndiye amene amadzetsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi. Amang'animitsa mphezi za mvula, amakunthitsa mphepo kuchokera kumene amaisunga. Anthu onse ndi opusa, alibe nzeru. Mmisiri aliyense wosula amachita manyazi ndi mafano ake. Mafano amene amapangawo ngabodza, mwa iwo mulibe konse moyo. Mafanowo ngachabechabe, oyenera kuŵaseka, ndipo pamene anthuwo adzalangidwe, mafanowo adzaonongedwa. Koma Mulungu wa Yakobe sali ngati mafanowo, Iye ndiyedi Mlengi wa zonse. Aisraele ndi anthu ake amene Iye adaŵasankha, dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse. Iwe Babiloni ndiwe nyundo yanga, chida changa chankhondo: ndi iwe ndimaphwanyaphwanya mitundu ya anthu, ndimaononga maufumu. Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya akavalo ndi okwerapo ao. Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya magaleta ndi oyendetsa ake. Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya amuna ndi akazi ao. Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya nkhalamba ndi achinyamata. Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya anyamata ndi anamwali. Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya abusa ndi ziŵeto zao. Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya alimi ndi ng'ombe zao. Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya abwanamkubwa ndi atsogoleri ankhondo. “Inu mukupenya, ndidzalipsira Babiloni ndi onse okhalamo chifukwa cha zolakwa zonse zimene adachita ku Ziyoni,” akutero Chauta. “Ndikukuimba mlandu, iwe phiri loononga, iwe amene umasakaza dziko lonse lapansi. Ndidzasamula dzanja langa pofuna kukulanga, ndi kukugubuduzira kunsi kuchokera pa mathanthwe ako. Ndidzakusandutsa phiri lopserera. Palibe mwala wako ndi umodzi womwe umene adzabwere nawo kuti augwiritse ntchito ngati mwala wapangodya. Iwe udzakhala chipululu mpaka muyaya,” akutero Chauta. “Kwezani mbendera yankhondo pa dziko, lizani lipenga kuti mitundu ya anthu imve. Itanani mitundu yonse kuti imuthire nkhondo Babiloni. Itanani maufumu a ku Ararati, a ku Mini ndi a ku Asikenazi. Ikani mtsogoleri wankhondo kuti amenyane ndi Babiloniyo. Mubweretse akavalo ochuluka ngati dzombe. Sonkhanitsani mitundu ya anthu kuti imuthire nkhondo. Muitane mafumu a ku Medi, pamodzi ndi abwanamkubwa ndi nduna zao, ndiponso ankhondo a m'maiko onse amene amaŵalamulira. Dziko likunjenjemera, likuphiriphitha chifukwa cha kupweteka, chifukwa zimene Chauta adakonzera Babiloni zidzachitikadi, zakuti adzamsandutsa dziko lachipululu lopanda anthu. Ankhondo a ku Babiloni aleka kuponya nkhondo, angokhala khale m'malinga ao. Mphamvu zao zatha, asanduka ngati akazi. Nyumba zake zatenthedwa, mipiringidzo ya zipata zake yathyoka. Othamanga akungopezanapezana, amithenganso akungotsatanatsatana. Onsewo akukauza mfumu ya ku Babiloni kuti mbali zonse za mzinda wake zalandidwa. Madooko onse alandidwa, malo obisalako alonda atenthedwa, ndipo ankhondo ake onse asokonezeka. Babiloni wokongola uja wangokhala ngati popunthira tirigu pa nthaŵi yopuntha kumene. Ndipotu posachedwa nthaŵi yake yokolola ifika,” akutero Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele. A ku Yerusalemu akuti, “Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, watiwononga, Watitswanya ndi kutitaya ngati mbiya yopanda kanthu. Watimeza ngati ng'ona. Wakhuta ndi zakudya zathu zotsekemera, kenaka nkutilavula.” Anthu okhala m'Ziyoni anene kuti, “Zankhanza zimene Ababiloni adatichita ife ndi ana athu ziŵabwerere.” Anthu okhala mu Yerusalemu anene kuti, “Magazi athu amene adamwazika aŵagwere Ababiloniwo ngati chilango chao.” Nchifukwa chake Chauta akunena kuti, “Ndidzakumenyera nkhondo yako, ndipo ndidzakulipsirira. Ndidzaumitsa nyanja ya ku Babiloni, akasupe ake onse adzaphwa. Motero Babiloni adzasanduka mulu wa nyumba zopasuka, malo a nkhandwe, malo oopsa ndi onyozeka, opanda wina wokhalamo. “Ababiloni adzakhuluma ngati mikango. Adzadzuma ngati ana a mikango. Akachita dyera, ndidzaŵakonzera madyerero. Tsono ndidzaŵaledzeretsa, ndipo adzasangalala nkugona tulo tampakampaka, osadzukanso ai. Ndidzapita nawo kuti akaphedwe ngati anaankhosa, ngati nkhosa zamphongo kapena atonde,” akutero Chauta. “Ndithu Babiloni wagonjetsedwa, mzinda umene dziko lonse lapansi linkaunyadira walandidwa. Ogo! Babiloni uja wasanduka chinthu chonyansa pakati pa mitundu ya anthu! Nyanja yakwera mpaka kumiza Babiloni, waphimbidwa ndi mafunde ake. Mizinda yake yasanduka malo onyansa, dziko louma ndi lachipululu, dziko lopanda anthu losayendako mwanawamunthu. Ndidzalanga Beli, mulungu wa Ababiloni, ndidzamsanzitsa zimene adameza. Mitundu ya anthu sidzapitanso kwa iye. Malinga a Babiloni agwa! Tulukani m'Babiloni, inu anthu anga! Fulumirani, pulumutsani moyo wanu! Thaŵani mkwiyo woopsa wa Chauta! Musataye mtima. Musaope maphephe amene awanda m'dziko monse. Chaka ndi chaka pamabuka ndithu maphephe onena za nkhondo pa dziko lapansi, ndiponso zakuti mfumu yakutiyakuti ikumenyana ndi inzake. “Tsono ikudza nthaŵi pamene ndidzalange mafano a Babiloni. Dziko lonselo lidzachita manyazi. Anthu ake onse ophedwa adzakhala ali ngundangunda pakati pake. Pambuyo pake dziko lakumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zokhala m'menemo zidzaimba mokondwera chifukwa cha kugwa kwa Babiloni. Anthu oononga ochokera kumpoto adzamgonjetsa,” akutero Chauta. Babiloni ayeneradi kugwa chifukwa cha amene adaphedwa ku Israele, monga adagwera anthu a pa dziko lonse lapansi amene adaphedwa ndi iyeyo. “Inu amene mwapulumuka ku nkhondo ya Babiloni, chokanipo apa, musazengereze. Kumbukirani Chauta ngakhale muli kutali ndi kwanu, muzimkumbukira Yerusalemu. Inu mukuti ‘Tikuchita manyazi chifukwa cha manyozo amene talandira. Nkhope zathu zagwa chifukwa anthu achilendo aloŵa ku mabwalo opatulika a ku Nyumba ya Chauta.’ ” Koma Chauta akunena kuti, “Ikubwera nthaŵi pamene ndidzalange mafano a ku Babiloni, ndipo kubuula kwa anthu olasidwa kudzamveka m'dziko lake lonse. Ngakhale Babiloni adzikweze mpaka ku mlengalenga, nkulimbitsa nsanja zake, ndidzatuma oononga kuti amgonjetse,” akutero Chauta. “Imvani mau olira m'Babiloni. Imvani phokoso la kuwonongeka kwakukulu m'dziko la Ababiloni. Ndithu, Chauta akuwononga Babiloni, ndipo akuthetsa phokoso lake lalikulu. Mfuu wa anthu ake ukumveka ngati mafunde amkokomo, phokoso lake likukwererakwerera. Woononga amufikira Babiloni, ndipo ankhondo ake onse agwidwa, mauta ao athyoka. Pajatu Chauta ndi Mulungu wolanga, adzabwezeradi kwathunthu zoipa zao. Ndidzaledzeretsa akuluakulu ake pamodzi ndi anzeru ake. Ndidzaledzeretsa abwanamkubwa ake, atsogoleri ankhondo, ndi ankhondo ake amene. Adzagona tulo tampakampaka, tosadzuka nato,” ikutero mfumu imene dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse. Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Malinga aakulu a Babiloni adzasalazidwa. Zipata zake zazitali zidzatenthedwa. Mitundu ya anthu idagwira ntchito pachabe, anthu adangotopa nkumanga zimene tsopano zikupsa ndi moto.” Mfumu Zedekiya anali ndi phungu wake wamkulu, dzina lake Seraya, mwana wa Neriya, mdzukulu wa Maseiya. Pa chaka chachinai cha ufumu wa Zedekiya ku Yuda, Seraya adatsagana ndi mfumuyo kupita ku Babiloni. Tsono mneneri Yeremiya adampatsirako uthenga Serayayo. Yeremiya anali atalemba m'buku za chiwonongeko chonse cha Babiloni, ndiponso za zina zonse zokhudza Babiloni. Yeremiyayo adauza Seraya kuti, “Pamene ukafike ku Babiloni, usakalephere kuŵaŵerengera anthu mau onseŵa. Ukanene kuti, ‘Inu Chauta, mwalengeza cholinga chanu chofuna kuwononga malo ano, osasiyapo kanthu, munthu kapena nyama. Ndipo adzakhala chipululu mpaka muyaya.’ Ukakatha kuŵerenga bukulo, ukalimangire ku mwala, nkuliponya mu mtsinje wa Yufurate. Ndipo ukanene kuti, ‘Umu ndimo m'mene Babiloni adzamirire. Sadzadzukanso chifukwa cha zoopsa zonse zimene ndidzamgwetsere.’ ” Mau a Yeremiya athera pamenepa. Zedekiya anali wa zaka 21 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka khumi ndi chimodzi ku Yerusalemu. Mai wake anali Hamutala, mwana wa Yeremiya wa ku Libina. Zedekiyayo adachita zoipa pamaso pa Chauta potsata zonse zimene ankachita Yehoyakimu. Chifukwa cha zonse zimene zidachitika ku Yerusalemu ndi ku Yudazi, Chauta adakwiya kwambiri, mpaka kuŵachotsa anthuwo pamaso pake. Tsono Zedekiya adapandukira mfumu ya ku Babiloni. Ndiye pa chaka chachisanu ndi chinai cha ufumu wa Zedekiyayo, mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adabwera ndi ankhondo ake onse kudzathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu. Adauzinga ndi zithando zankhondo ponseponse. Motero mzindawo udaazingidwa ndi zithandozo mpaka chaka cha 11 cha ufumu wa Zedekiya. Tsono pa tsiku lachisanu ndi chinai, pa mwezi wachinai wa chaka chimenecho, pamene njala inali itakula kwambiri mumzindamo kotero kuti anthu analibiretu chakudya m'dzikomo, malinga a mzindawo adabooledwa. Pamenepo ankhondo onse adathaŵa mumzindamo usiku, kutulukira pa chipata cha pakati pa makoma aŵiri, pafupi ndi munda wa mfumu, ngakhale kuti Ababiloni anali atauzinga mzindawo. Ndipo adathaŵira ku Araba. Koma gulu lankhondo la Ababiloni lidamlondola mfumu Zedekiya nkukamgwirira m'zigwa za ku Yeriko. Ankhondo ake adabalalika namsiya. Apo a ku Babiloni aja atamgwira Zedekiya, adapita naye kwa Nebukadinezara, ku Ribula m'dziko la Hamati. Komweko Nebukadinezarayo adagamula mlandu wa Zedekiya uja. Pompo adapha ana a Zedekiya iyeyo akupenya. Adaphanso akalonga onse a ku Yuda ku Ribula komweko. Ndipo adamkolowola maso Zedekiyayo, nammanga ndi maunyolo nkupita naye ku Babiloni. Kumeneko adamuponya m'ndende kuti akhalemo moyo wake wonse. Mwezi wachisanu, pa tsiku lakhumi la mwezi, chaka cha 19 cha ufumu wa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, Nebuzaradani, mkulu wa asilikali oteteza mfumu, mmodzi wa aphungu ake, adadza ku Yerusalemu. Ndipo adatentha Nyumba ya Chauta, nyumba ya mfumu, ndi nyumba zina zonse za ku Yerusalemu, nyumba yaikulu iliyonse adaitentha. Tsono gulu lonse lankhondo la ku Babiloni limene linali ndi mkulu wa asilikali uja, lidagumula malinga onse ozinga Yerusalemu. Anthu ena onse amene adaatsala mumzindamo, ndi ena amene adaadzipereka kale kwa mfumu ya ku Babiloni, pamodzi ndi anthu aluso otsala, Nebuzaradani mkulu wa asilikali uja adaŵatenga kupita nawo ku Babiloni. Koma Nebuzaradani adasiyako anthu ena osauka kwambiri am'dzikomo, kuti azilima minda ya mphesa ndi minda ina. Ankhondo a ku Babiloni adaphwanya nsanamira zamkuŵa za m'Nyumba ya Chauta, ndiponso maphaka ndi chimbiya chamkuŵa, ndipo adatenga mkuŵa wonsewo, napita nawo ku Babiloni. Ankhondowo adachotsanso mbiya, zoolera phulusa, zozimira nyale, mbale zofukizira lubani, zikho kudzanso ziŵiya zonse zamkuŵa zimene ankagwiritsira ntchito ku Nyumba ya Chauta. Mkulu wa Asilikali uja adatenga mabeseni, ziwaya zosonkhapo moto, mbale zowazira madzi, zoikapo nyale, zipande zofukizira lubani ndi zikho, ndi zina zonse zagolide ndi zasiliva. Nsanamira ziŵiri zija, chimbiya, maphaka ndiponso ng'ombe zamphongo khumi ndi ziŵiri zimene zinkachirikiza chimbiyacho, zimene mfumu Solomoni adaapangira Nyumba ya Chauta kulemera kwake kwa mkuŵa wa zonsezo kunali kosaŵerengeka. Nsanamira imodzi kutalika kwake inali mamita asanu ndi atatu, kuzungulira kwake inali mamita asanu ndi theka. Inali ndi chiboo m'kati, ndipo kuchindikira kwake inali zala zinai. Inali ndi mutu wamkuŵa, kutalika kwake mamita aŵiri. Pozungulira mutuwo panali ukonde ndi makangaza, zonsezo zamkuŵa. Nsanamira inayo inalinso ndi makangaza ndipo inkafanana ndi inzakeyo pa zonse. Makangaza 96 anali pambali, koma onse pamodzi analipo zana limodzi, kuzungulira ukonde wonsewo. Tsono Nebuzaradani mkulu wa asilikali uja, adagwira Seraya mkulu wa ansembe ndi Zefaniya, wachiŵiri kwa mkulu wa ansembe, ndi alonda atatu apachipata. Mumzindamo adagwiramo mkulu amene ankalamulira ankhondo, ndiponso anthu asanu ndi aŵiri amene anali aphungu a mfumu mumzindamo. Adagwiranso mlembi wa mtsogoleri wa ankhondo, amene ankalemba anthu am'dzikomo, ndiponso akuluakulu ena 60, amene anali mumzindamo. Nebuzaradani, mkulu wa asilikali uja, adaŵatenga onsewo napita nawo kwa mfumu ya ku Babiloni ku Ribula. Mfumu ya ku Babiloni idalamula kuti onsewo aphedwe ku Ribula m'dziko la Hamati. Motero anthu a ku Yuda adatengedwa ukapolo kuŵachotsa kutali ndi dziko lao. Nachi chiŵerengero cha anthu amene Nebukadinezara adaŵatenga ukapolo. Pa chaka chachisanu ndi chiŵiri cha ufumu wake, adatengedwa Ayuda 3,023. Pa chaka cha 18 cha ufumu wake, Nebukadinezara adatenga ukapolo anthu 832 kuchokera ku Yerusalemu. Pa chaka cha 23 cha ufumu wa Nebukadinezara, Nebuzaradani mtsogoleri wa alonda oteteza mfumu uja adatenga ukapolo Ayuda 745. Onse pamodzi otengedwa ukapolo adakwanira 4,600. Pa chaka cha 37 cha ukapolo wa Yehoyakimu, mfumu ya ku Yuda, tsiku la 25 la mwezi wa 12, Evili-Merodaki, mfumu ya ku Babiloni adangoti ataloŵa ufumu, adakomera mtima Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda, namtulutsa m'ndende. Adalankhula naye mwachifundo, nampatsa malo aulemu kuposa mafumu ena amene anali naye ku Babiloni. Motero Yehoyakimu adavula zovala zake zakundende, ndipo tsiku ndi tsiku ankadya ndi mfumu pa moyo wake wonse. Kunena za phoso, mfumu ya ku Babiloni inkampatsa Yehoyakimu phoso lake tsiku ndi tsiku mpaka kufa kwake. Ha! Mzinda wa Yerusalemu wakhala wokhawokha, m'menemo kale udaali wodzaza ndi anthu! Kale unali wotchuka pakati pa mitundu ya anthu, koma tsopano wasanduka ngati mkazi wamasiye. Kale unali mzinda wolemekezeka koposa mizinda ina, koma tsopano wasanduka kapolo. Ukungolira usiku wonse, misozi ikungoti mbwembwembwe pamasaya pake. Mwa onse amene ankaukonda, palibe ndi mmodzi yemwe amene watsala woti aziwusangalatsa. Abwenzi ake onse auchita zaupandu, onse asanduka adani ake. Ayuda apita ku ukapolo kukazunzika, ndi kukagwira ntchito yakalavulagaga. Akukhala m'maiko ena, osaona malo opumulira. Onse oŵapirikitsa aŵapeza, ali pa mavuto zedi. Miseu yopita ku Ziyoni yaŵirira, chifukwa palibe wopitako kuti akapembedze pa masiku achikondwerero. Zipata zake zonse zili pululu, ansembe ake akungodandaula. Anamwali ake aja mtima wao ukupweteka, ndithu Ziyoni ali pa masautso oopsa. Adani ake asanduka omulamulira, odana naye akupeza bwino, popeza kuti Chauta wamugwetsa m'mavuto chifukwa cha machimo ochuluka a anthu ake. Ana ake amuchokera, atengedwa ukapolo ndi adani. Ulemerero wonse wa Ziyoni wachokeratu. Akalonga ake asanduka ngati mphoyo zosoŵa msipu. Ankathaŵa opanda ndi mphamvu zomwe, pofika adani. Pa masiku a mavuto ake ndi a kuzunzika kwake, Yerusalemu amakumbukira zabwino zonse zimene anali nazo masiku amakedzana. Pamene anthu ake adagwa m'manja mwa adani, panalibe womuthandiza. Adani ake ankamupenyetsetsa monyodola namaseka kugwa kwake. Yerusalemu adachimwa kwambiri, motero wasanduka wonyansa. Onse amene ankamulemekeza, akumunyoza tsopano, chifukwa aona maliseche ake. Iyeyo akungobuula ndipo akuyang'ana kumbali. Uve wake unkaonekera poyera, iye osaganizako za tsoka lake lakutsogolo. Nchifukwa chake kugwa kwake kunali koopsa, ndipo panalibe womuthuzitsa mtima. Akungoti, “Inu Chauta, muyang'ane mavuto anga, pakuti adani anga apambana.” Adani adamulanda chuma chake chonse. M'malo ake oyera mudaloŵa anthu a mitundu ina, amene Inu Chauta mudaŵaletsa kuloŵa mumsonkhano mwanu. Anthu ake onse amabuula akamafunafuna chakudya. Chuma chao amagulitsana ndi chakudya, kuti apezenso mphamvu. Akuti, “Inu Chauta penyani, muwone m'mene akundinyozera.” Kodi zimenezi mukuziyesa zachabe, inu amene mukudutsanu? Tangopenyani, muwone ngati pali mavuto ena onga angaŵa, mavuto amene Chauta adandigwetsamo, pamene adandikwiyira koopsa. Adatumiza moto kuchokera Kumwamba. Udaloŵa mpaka m'kati mwa mafupa anga. Adayala ukonde kuti akole mapazi anga, nandibweza. Adandisiya ndili ndi chisoni chachikulu, ndili wolefuka tsiku lonse. Zolakwa zanga adazimanga pamodzi kuti zikhale ngati goli. Adazimanga ndi manja ake. Adazimangirira m'khosi mwanga, adafooketsa mphamvu zanga. Chauta wandipereka kwa anthu amene sindingathe kulimbana nawo. Chauta adaŵamwaza anthu anga onse amphamvu amene ankakhala nane. Adasonkhanitsa gulu lina la anthu kuti liwononge anyamata anga. Chauta adapondereza Ayuda, anthu ake opatulika, monga m'mene anthu amachitira mphesa mopondera mwake. Chifukwa cha zimenezi ndikulira, misozi ili mbwembwembwe m'masomu. Pakuti wondisangalatsa sali pafupi, wondilimbitsa mtima ali kutali. Anthu anga asiyidwa chifukwa mdani watigonjetsa. Ziyoni wakweza manja, koma palibe ndi mmodzi yemwe womusangalatsa. Chauta adalamula kuti Yakobe anansi ake asanduke adani ake. Yerusalemu wasanduka chinthu chonyansa pakati pao. Pamenepo Chauta wakhoza, chifukwa ndine ndidapandukira malamulo ake. Imvani, inu anthu a mitundu yonse, onani kuvutika kwanga. Anamwali anga ndi anyamata anga atengedwa ukapolo. Ndidaitana abwenzi anga, koma iwo adanditaya. Ansembe anga ndi akuluakulu anga adafa mu mzinda, pamene ankafunafuna chakudya kuti mphamvu zao zibwereremo, Onani Inu Chauta m'mene ndavutikira mumtima mwanga, moyo wanga wazunzika zedi. Mtima wanga wakongonyala, chifukwa choti ndapanduka kwambiri. Mu mseu anthu akuphedwa ndi lupanga, m'nyumbanso ndi imfa yokhayokha. Anthu akundimva pamene ndikudandaula, koma palibe wondisangalatsa. Adani anga onse atamva za tsoka langa, adakondwa chifukwa cha zimene mudachita. Tsiku limene mudalonjeza lija mulifikitse ndithu. Nawonso adzasauke ngati ine ndemwe. Ntchito zao zonse zoipa mudzaŵaimbe nazo mlandu. Muŵalange monga mudandilangira ine chifukwa cha zolakwa zanga zonse. Ndikubuula kwambiri, ndipo mtima wanga wafookeratu. Chauta wakwiya kwambiri, taonani m'mene waphimbira Ziyoni ndi mdima! Ulemerero wa Israele wautaya pansi kuuchotsa Kumwamba. Pa tsiku la mkwiyo wake sadakumbukirenso kuti Ziyoni anali ngati mphondero yake. Chauta adaononga midzi yonse ya Yakobe popanda ndi chifundo chomwe. Chifukwa cha kupsa mtima adathyola malinga a mizinda ya Yuda. Adagwetsera pansi mochititsa manyazi, ufumu wa Israele ndi olamulira ake. Chauta atapsa mtima adathyola nyonga zomwe ankanyadira Israele. Adabweza dzanja lake loteteza, adani atayandikira. Mkwiyo wake udalanga fuko la Yakobe ngati moto walaŵilaŵi wonka nuwononga zonse. Adalozetsa mivi yake kwa ife ngati mdani wathu, wasamuladi dzanja ngati mdani. Adapha onse amene tinkaŵayang'ana monyadira, pakati pa anthu a mu mzinda wa Ziyoni. Ukali wake unkachita kuyaka ngati moto. Chauta adakhala ngati mdani, adaononga Israele. Adaononga nyumba zonse zachifumu, malinga ao onse adaŵasandutsa mabwinja. Adachulukitsa kulira ndi kudandaula pakati pa anthu a ku Yuda. Adapasula Nyumba yake ngati khumbi lam'munda, malo ake a msonkhano adaŵasandutsa bwinja. Chauta adathetseratu ku Ziyoni masiku achikondwerero ndi a Sabata. Ndipo atakwiya kwambiri adanyoza mfumu pamodzi ndi ansembe. Chauta adanyoza ngakhale guwa lake lomwe, ndipo adaŵakana malo ake opatulika. Adapereka malinga a nyumba zake zachifumu m'manja mwa adani ake. M'nyumba yeniyeni ya Chauta adaniwo adafuula ndi chimwemwe monga momwe zimachitikira pa tsiku lachikondwerero. Chauta adaatsimikiza zoti aononge malinga a mzinda wa Ziyoni. Adauyesa ndi chingwe chake, ndipo sadafune kuleka kuuwononga kotheratu. Adaliritsa okhala pa malinga ndi pa makoma ake, onsewo akuzunzikira limodzi. Zipata za mzindawo zakwiririka pansi. Mipiringidzo yake yathyoka ndi kusakazika. Mfumu yake ndi akalonga ake ali ku ukapolo pakati pa anthu akunja, malamulo a Mulungu palibenso oŵalalika. Aneneri ake omwe sakuchitanso zija zoona zinthu m'masomphenya zochokera kwa Mulungu. Akuluakulu a mu mzinda wa Ziyoni, akhala pansi atangoti chete. Adzithira fumbi kumutu, ndipo avala ziguduli. Anamwali a ku Yerusalemu aŵeramitsa mitu yao pansi. Maso anga atopa nkulira, moyo wanga wazunzika zedi, Mumtima mwanga mwadzaza chisoni, chifukwa choti anthu anga aonongeka, ana ndi makanda omwe akukomoka m'miseu yamumzinda. Anawo akufunsa amai ao kuti, “Kodi chakudya ndi chakumwa tingazipeze kuti?” Akufunsa zimenezi pamene akukomoka m'miseu yamumzinda ngati anthu olasidwa. Akuthatha ndi moyo pa mfukato wa amai ao. Iwe mzinda wa Yerusalemu, ndinganene chiyani za iwe, kaya nkukuyerekeza ndi chiyani? Iwe mzinda wangwiro wa Ziyoni, kodi ndingakufanizire ndi yani, kuti choncho ndikusangalatse? Kuwonongeka kwako nkwakukulu ngati nyanja. Ndani angathe kukukonzanso? Zinthu zimene aneneri ako adakuwonera m'masomphenya zinali zabodza ndi zonyenga. Iwo sadaonetse uchimo wako, kuti ukhalenso pabwino. Mau amene adakutengeraniwo anali abodza ndi osokeretsa. Onse odutsa m'njira akukuwombera m'manja mokunyodola. Akukutsonya ndi kukupukusira mitu, iwe mzinda wa Yerusalemu. Akunena kuti, “Kodi mzinda uja ndi uwu umene kale lija ankautcha wodala kotheratu, mzinda wokondweretsa dziko lonse lapansi?” Adani ako onse akukuyasamira kukamwa mwaukali, ndipo akukunyodola. Akukutsonya ndi kumakukuta mano ao namanena kuti, “Tafikapodi pousakaza! Ah! Tsiku lija tinkafunali ndi lero. Tagonera, taliwonadi.” Chauta wachitadi zimene adakonzekera kuti achite. Wachitadi zimene ankanena moopseza. Monga momwe adaakonzeratu masiku amakedzana, wakuwononga mopanda chifundo, walola adani kuti akondwe chifukwa cha tsoka lako, ndipo wakulitsa kwambiri mphamvu za adani ako. Fuulani kwamphamvu kwa Ambuye, inu anthu a ku Ziyoni. Misozi yanu ichite kuti yoyoyo, ngati mtsinje, usana ndi usiku. Musadzipatse nthaŵi yoti mupumule. Misozi yanu isalekeze. Dzukani, ndipo mufuule usiku pachiyambi penipeni pa maulonda. Nenani zanu zonse zakukhosi pamaso pa Ambuye. Kwezani manja ndi kupemphera kwa Ambuyewo chifukwa cha moyo wa ana anu amene akukomoka ndi njala m'miseu yonse. Inu Chauta onani, ndipo mupenye! Kodi ndani amene Inu mwamuvuta chotereyu? Kodi akazi achite kudya ana ao, ana amene iwo omwe adaŵalera bwino? Nanga ansembe ndi aneneri, kodi achite kuŵaphera m'malo opatulika a Ambuye? Anyamata ali gonegone m'miseu pamodzi ndi nkhalamba zomwe. Anamwali anga ndi anyamata anga aphedwa ndi nkhondo. Mwaŵapha pa tsiku la mkwiyo wanu, mwaŵapha mopanda chifundo. Monga momwe mumaitanira ku chikondwerero, ndi m'mene mwandiitanira zoopsa kuchokera mbali zonse. Inu Chauta, pa tsiku la mkwiyo wanu, palibe amene adathaŵako kapena kupulumuka. Onse amene ndidaŵabala ndi kuŵalera, adani anga adaŵaononga. Ine ndine munthu amene ndaona mavuto, ndalangidwa ndi ndodo ya ukali wa Mulungu. Adandiyendetsa ndi kubwera nane mu mdima mopanda nkuŵala komwe. Zoonadi adandikantha ndi dzanja lake, ankachita zimenezi mobwerezabwereza tsiku lonse. Adandipweteka m'thupi lonse, ndipo adaphwanya mafupa anga onse. Adandizinga ndi kundizunguliza ponseponse ndi mazunzo ndi masautso. Adanditaya m'malo a mdima wabii, kuti ndikhale ngati munthu wofa kalekale. Adanditsekera m'malinga kuti ndisathaŵe. Adandimanga ndi maunyolo olemera kwambiri. Ngakhale pamene ndinkafuula ndi kupempha chithandizo, sankalimva pemphero langalo. Adanditsekera mseu ndi miyala yosema, ndipo adakhotetsa njira zanga. Adandiwukira ngati chimbalangondo kapena ngati mkango wondilalira. Adandisiyitsa njira nanding'ambang'amba, kenaka nkundisiya. Adakoka uta wake nandiyesa chinthu chochitirapo chandamale. Adalasa mtima wanga ndi mivi ya m'phodo lake. Ndasanduka chinthu chomachiseka, kwa anthu a mitundu ina, amandiimba nyimbo zondinyoza. Chauta adandidyetsa zoŵaŵa, adandimwetsa chivumulo. Adandigulula mano ndi timiyala, adandivimviniza m'phulusa. Mumtima mwanga mulibenso mtendere, chimwemwe ndidachiiŵaliratu. Choncho ndikuti, “Ulemerero wanga wonse watha, chandithera chikhulupiriro cholandira kanthu ka Chauta.” Ndimakumbukira masautso anga ndi kuzunzika kwanga, zili ngati chivumulo ndi ndulu. Nthaŵi zonse ndimangozilingalirabe zimenezi, nkuwona ndataya mtima. Koma pali chinanso chimene ndimachikumbukira, chimenecho ndicho chimandilimbitsa mtima. Chikondi chosasinthika cha Chauta sichitha, chifundo chakenso nchosatha. M'maŵa mulimonse zachifundozo zimaoneka zatsopano, chifukwa Chauta ndi wokhulupirika kwambiri. Chauta ndiye zanga zonse motero ndimadalira Iyeyo. Chauta ndi wabwino kwa amene amamudalira, kwa onse amene amafuna kuchita zimene Iye afuna. Nkwabwino kumdikira Chauta mopirira kuti aonetse chipulumutso chake. Nkwabwinonso kuti munthu asenze goli la kupirira pamene iye ali pa unyamata. Akhale pansi yekha mkachete, pamene Chauta amsenzetsa golilo. Agwetse nkhope yake pa fumbi, mwina chikhulupiriro nkukhalapobe. Apereke tsaya lake kwa wofuna kumumenya, apirire zomunyoza zonse. Ndithudi Ambuye sadzataya atumiki ao mpaka muyaya. Angathe kulanga mwankhalwe, komabe adzaonetsa chifundo, chifukwa chikondi chao nchochuluka. Savutitsa mwadala, sakonda kusautsa munthu aliyense. Chauta amadziŵa pamene akulu amapondereza am'ndende am'dziko. Amadziŵa pamene olamula amapsinja munthu popanda chilungamo pamaso pa Wopambanazonse. Pamene iwo amagamula mlandu mokondera, kodi Ambuye saona zimenezi? Ndani angathe kulamula kuti zakutizakuti zichitike, ngati Chauta waletsa zimenezo? Paja madalitso ndi matsoka zonse nzochokera kwa Wopambanazonse. Munthu wina aliyense wamoyo angadandaulirenji pamene alangidwa chifukwa cha machimo ake? Tiyeni tiŵaone ndi kuŵayesa makhalidwe athu, ndipo tibwerere kwa Chauta. Tikweze mitima yathu ndi manja athu kwa Mulungu kumwamba. Ifeyo tachimwa, ndipo tapanduka, tsono Inu simudakhululuke. Mwatipirikitsa muli okwiya, ndipo mwatipha mopanda chifundo. Mwadzibisa ndi mitambo, kumene mapemphero athu sangathe kufikako. Mwatisandutsa onyozeka ngati zinyatsi, m'maso mwa anthu a mitundu ina. Adani athu akutinyodola. Tagwa m'zoopsa ndi m'mbuna, m'chipasupasu ndi m'chiwonongeko. M'maso mwanga misozi ikungoti mbwembwembwe, chifukwa anthu anga aonongeka. Ndidzalira misozi kosalekeza ndiponso osapumulira, mpaka Chauta adzayang'ane pansi kuchokera kumwamba ndi kuwona mavuto anga. Mtima wanga ukupweteka poona zimene zikuŵachitikira akazi a mumzinda mwanga. Amene anali adani anga popanda chifukwa, akhala akundisaka ngati mbalame. Adandiponya m'dzenje ndili moyo, nkumandiponya miyala ndili momwemo. Madzi adaamiza mutu wanga, ine nkunena ku, “Mayo, ndikufa ine!” Ndidatama dzina lanu mopemba, Inu Chauta, ndili m'dzenje lozamalo. Inu mudamva mau anga akuti, “Musagonthetse dala makutu anu pamene ndikupemphera kuti mudzandithandize.” Inu mudasendera pafupi pamene ndinkakutamani mopemba, ndipo mudanena kuti “Usachite mantha.” Inu Chauta, mudandithandiza pa mlandu wanga, ndipo mudaombola moyo wanga. Inu Chauta, mudaona zoipa zimene anthu adandichita, tsono muweruze ndinu pamenepo. Mudaona m'mene ankandilipsirira, mudaonanso ziwembu zimene adandichita. Inu Chauta mudamva kunyoza kwao koopsa ndiponso ziwembu zimene ankakonzekera kuti andichite. Mudamva manong'onong'ono ao, ndi m'mene adani anga ankandinenera tsiku lonse. Onani m'mene akundinyozera, m'maŵa ndi madzulo akungokhalira kundiimba nyimbo. Inu Chauta, muŵalange potsata zolakwa zao, potsata ntchito zimene adachita. Muŵazamitse mtima muŵatemberere basi. Inu Chauta, muŵapirikitse mwaukali, muŵaonongeretu pa dziko lapansi. Ha! Golide wathu tsopano wathimbirira kwambiri. Golide wathu wosalala uja wasinthika kotheratu. Miyala ya ku malo oyera yamwazikana, ili vuu, ku mphambano zonse za miseu. Onani ana okondedwa a m'Ziyoni amene kale anali ngati golide kwa ife, tsopano akuŵayesa mbiya zadothi zimene woumba amachita kuumba ndi manja ake. Ngakhale nkhandwe siziwumira bere, zimayamwitsa ana. Koma anthu anga ndi ankhalwe, ali ngati nthiŵatiŵa zakunkhalango. Lilime la mwana wakhanda limakangamira kukhosi chifukwa cha ludzu. Ana aang'ono amafuna chakudya, koma palibe woŵapatsa mpang'ono pomwe. Amene ankadya zokoma akuthera m'miseu. Amene ankavala zokongola zokhazokha tsopano ali gone pa dzala. Chilango cha anthu anga nchachikulu kwambiri kupambana chilango cha anthu a ku Sodomu, amene adalangidwa pa kamphindi chabe, ndipo panalibe wochitapo kanthu kuti aŵathandize. Akalonga ake anali oŵala koposa chisanu chambee, oyera kuposa mkaka. Matupi ao anali ofiira kupambana miyala ya rubi. Anali ndi maonekedwe okongola ngati miyala ya safiro. Koma tsopano nkhope zao zasanduka zakuda ngati mwaye. Palibe amene akuŵazindikira m'miseu. Khungu lao lachita makwinyamakwinya, langoti gwa ngati mtengo. Amene adaphedwa pa nkhondo anali amwai kwambiri kupambana amene adafa ndi njala. Ameneŵa ankafooka pang'onopang'ono mpaka kutsirizika, chifukwa chosoŵa chakudya. Ngakhale akazi achifundo ndi manja ao omwe adafika pophika ana ao. Ana aowo adasanduka chakudya chao pa nthaŵi imene anthu anga adaonongedwa. Chauta adakwiya kwambiri, nagwetsa pansi mkwiyo wake wamotowo. Adayatsa moto ku Ziyoni ndipo motowo udaononga maziko a mzindawo. Mafumu a pa dziko lapansi sadakhulupirire, kapena wina aliyense wokhala pa dziko lapansi, kuti adani kapena ankhondo nkuloŵa pa zipata za Yerusalemu. Zimenezi zidachitika chifukwa cha machimo a aneneri ake ndi ntchito zoipa za ansembe ake, amene ankakhetsa magazi a anthu osalakwa m'malinga amumzindamu. Ankangoyendayenda m'miseu ngati akhungu, zovala zao zili magazi psu, mwakuti palibe munthu woti nkuzikhudza. Anthu ankaŵafuulira kuti, “Chokani, inu anthu oipitsidwa. Chokani! Chokani apa! Musakhudzane ndi ife!” Motero adathaŵa, namangoyendayenda, anthu a mitundu ina ankati, “Asadzakhalenso ndi ife.” Chauta mwiniwake ndiye adaŵamwaza, salabadakonso za iwo. Ansembe sadaŵalemekezenso. Akuluakulu sadaŵamvere chifundo. Maso athu adatopa nkuyang'anira chithandizo, koma popanda phindu. Tidadikiradikira mtundu wina wa anthu amene sangathe kutipulumutsa. Anthu ankangotilondola nthaŵi zonse, kotero kuti sitinkathanso kuyenda m'miseu yathu. Masiku athu ankacheperachepera, imfa yathu idaayandikira, ndithu chimalizo chinali chitafika. Anthu otilondolawo anali aliŵiro kupambana adembo ouluka mu mlengalenga. Adatipirikitsa ku mapiri, adatilalira ku chipululu kuti atiphe. Wodzozedwa wa Chauta uja, amene anali ngati mpweya wotipatsa moyo, adakodwa m'misampha mwao. Iyeyo amene tinkati adzatithandiza ife okhala pakati pa anthu a mitundu ina. Kondwerani ndipo musangalale, inu anthu a ku Edomu, inu anthu okhala m'dziko la Uzi. Inunso chikho cha mavuto chidzakufikirani pa nthaŵi yanu. Mudzaledzera mpaka kuvula zovala. Chilango cha machimo anu, inu anthu a ku Ziyoni, chatheratu, Chauta satalikitsa ukapolo wanu. Koma inu anthu a ku Edomu, Chauta adzakulangani chifukwa cha machimo anu. Zolakwa zanu adzaziwulula poyera. Inu Chauta, kumbukirani zimene zatigwera. Muyang'ane, muwone m'mene anthu akutinyozera. Choloŵa chathu chaperekedwa kwa alendo, nyumba zathu zili m'manja mwa anthu akudza. Ife tili ngati ana amasiye, opanda bambo wao. Amai athu ali ngati akazi amasiye. Madzi amene timamwaŵa tiyenera kuchita chogula. Nkhuni zosonkhera moto nzoyeneranso kuchita chogula. Amatikankha mwankhanza, goli lili m'khosi mwathu. Ngakhale titope, satilola kupumula. Tidachita chibwenzi ndi Aejipito ndiponso ndi Aasiriya, kuti mwina iwo nkutipatsako chakudya. Makolo athu adachimwa, ndipo adatha. Ndiye ife tatengana nacho chilango chifukwa cha machimo ao. Amene akutilamulira ndi akapolo, palibe ndi mmodzi yemwe wotipulumutsa m'manja mwao. Pofunafuna chakudya, timagwa m'zoopsa chifukwa cha anthu opha anzao ku chipululu. Khungu lathu likutentha ngati lili m'ng'anjo chifukwa cha ululu wa njala. Ku Ziyoni akazi akuŵachita zadama mwakhakhamizo. M'mizinda ina ya ku Yuda anamwali akuŵachita chimodzimodzi. Akalonga akuŵapachika pomangirira manja ao, akuluakulu sakuŵalemekeza konse. Achinyamata akuŵakakamiza kupera tirigu, anyamata akudzandira nayo mitolo ya nkhuni. Akuluakulu adachokapo pa bwalo la mzinda, achinyamata nyimbo zao zija zati zi! Chimwemwe chachoka m'mitima mwathu. Kuvina kwathu kwasanduka kulira. Chisoti chathu chaufumu chachoka kumutu, kugwa pansi. Tsoka kwa ife, chifukwa tachimwa. Nchifukwa chake mitima yathu yalefuka, chifukwa cha zimenezi m'masomu mwachita chidima. Phiri la Ziyoni lasanduka bwinja, nkhandwe zikungoyendayendapo. Koma Inu Chauta, ndinu mfumu mpaka muyaya, mpando wanu waufumu udzakhalapo pa mibadwo yonse. Chifukwa chiyani mwakhala mukutiiŵala nthaŵi yonse? Chifukwa chiyani mwatisiya nthaŵi yaitali chotere? Inu Chauta mutitembenuzire kwa Inu, kuti tibwerere mwakale. Mutipatsenso masiku onga amakedzana aja. Kaya, monga nkuti mwatitayiratu? Monga nkuti mwatikwiyira kopitirira? Tsiku lachisanu la mwezi wachinai, chaka cha 30, ndidaakhala pamodzi ndi akapolo a ku Yuda pafupi ndi mtsinje wa Kebara. Tsono Kumwamba kudatsekuka, ndipo ndidaona maonekedwe a Mulungu m'masomphenya. Linali tsiku lachisanu la mwezi, chaka chachisanu cha ukapolo wa mfumu Yehoyakini. Nthaŵi imeneyo Chauta adandipatsira uthenga ine Ezekiele, wansembe, mwana wa Buzi, m'mphepete mwa mtsinje wa Kebara, m'dziko la Ababiloni. Ndipo ndidamva mphamvu zake zikundifikira. Ndiyang'ane, ndidangomva mphepo yamkuntho yochokera kumpoto. Panali mtambo waukulu woŵala m'mphepete mwake monsemu, moto uli laŵilaŵi kuchokera mumtambomo. Pakati pake pa motowo pankaoneka ngati mkuŵa wochezimira. M'katikati mwa motowo ndidaona zinthu zokhala ngati zilengolengo zinai. Maonekedwe ake anali otere: thupili mapangidwe ake onga a munthu, koma chilichonse chinali ndi nkhope zinai ndi mapiko anai. Miyendo yake inali yoongoka, koma mapazi ake okhala ndi ziboda zonga za mwanawang'ombe. Zibodazo zinkaŵala ngati mkuŵa wonyezimira. M'munsi mwa mapiko ake, pa mbali zonse zinai, chilengolengo chilichonse chinali ndi manja a munthu. Zilengolengo zonsezo nkhope zake ndi mapiko ake zidaakhala motere: mapiko akewo anali okhudzana. Chilichonse poyenda chinkalunjika kutsogolo ndithu, osatembenuka popitapo. Nkhope zake zinkaoneka motere: chilichonse chinali ndi nkhope zinai zosiyana. Kutsogolo nkhope ya munthu, ku dzanja lamanja nkhope ya mkango, ku dzanja lamanzere nkhope ya ng'ombe, ndipo kumbuyo kwake nkhope ya chiwombankhanga. Ndimo m'mene zinaliri nkhope zake. Tsono mapiko ake anali otambasuka. Chilengolengo chilichonse chinali ndi mapiko aŵiri okhudzana ndi mapiko a chinzake. Chinalinso ndi mapiko aŵiri ena ophimbira thupi lake. Zilengolengozo poyenda zinkalunjika kutsogolo ndithu. Kulikonse kumene mzimu wake unkaziyendetsa, zinkapita kumeneko, osatembenuka popitapo. Pakati pake pa zilengolengozo panali chinthu chooneka ngati makala oyaka, kapena ngati miyuni yoyaka yomangoyendayenda pakati pake. Motowo unali woŵala zedi, ndipo m'kati mwake munkatuluka mphezi. Zilengolengozo zinkathamanga uku ndi uku ngati kung'anipa kwa mphezi. Tsono poyang'ana zilengolengo zija, ndidaona mikombero pansi, mkombero umodzi pambali pa chilengolengo chilichonse. Maonekedwe a mikomberoyo anali onga a mwala wonyezimira, ndipo inai yonseyo inali yolingana. Mapangidwe ake anali ngati kuti mikomberoyo idaloŵanaloŵana. Tsono poyenda inkatha kupita mbali iliyonse imene zilengolengozo zinkayang'ana, osachita kutembenuka. Mikombero inaiyo inali ndi marimu ataliatali ochititsa mantha. Marimuwo anali ndi maso pozungulira ponse. Zilengolengozo zinkati zikamayenda, mikomberoyo inkayendanso m'mbalimu. Zilengolengo zikamakwera m'mwamba, mikomberoyo inkakweranso. Kulikonse kumene mzimu wake unkaziyendetsa, zilengolengozo zinkapita kumeneko. Mikombero ija nayonso inkapita nazo pamodzi, chifukwa chakuti mzimu wa zilengolengozo ndiwo unkayendetsa mikomberoyo. Zilengolengo zinkati zikamayenda, mikombero inkayendanso. Zilengolengo zikaima, mikombero inkaimanso. Zilengolengo zikauluka, mikombero inkauluka nazo pamodzi. Pakuti mzimu wa zilengolengozo ndiwo unkayendetsa mikomberoyo. Pamwamba pa mitu ya zilengolengozo panali chinthu chonga thambo loŵala looneka ngati galasi lochezimira, loyalidwa pamwamba pa mitu yake. Zilengolengozo zidaatambalitsa mapiko ake m'munsi mwa thambo lija, mapiko ake ena kumakhudzana, mapiko aŵiri kumaphimbira thupili. Pamene zinkayenda, ndinkamva phokoso la mapiko ake ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati liwu la Mphambe kapena ngati phokoso la gulu lankhondo. Zikakhala chiimire, zinkagwetsa mapiko ake. Tsono pamwamba pa thambo la pa mitu yake padamveka phokoso, zilengolengozo zili chiimire choncho, mapiko akenso ali chigwetsere. Pamwamba pa thambo lija panali chinthu china chooneka ngati mpando waufumu, wopangidwa ndi mwala wa safiro. Pamwamba pa mpandowo panali chinthu chooneka ngati munthu. M'mwamba mwa chiwuno chake munali ngati chitsulo choŵala konsekonse ngati moto. M'munsi mwa chiwuno chake munalinso ngati moto wokhawokhawo. Kuŵala kwamphamvu kudaamzungulira munthuyo. Kuŵalako kunali ndi maonekedwe a utawaleza m'mitambo tsiku limene kwagwa mvula. Umu ndi m'mene ulemerero wa Chauta unkaonekera. Ndidangoti ntauwona, ndidadzigwetsa pansi chafufumimba, ndipo ndidamva mau ondilankhula. Mauwo adati, “Munthu iwe, imirira ndilankhule nawe.” Pamene ankalankhula, Mzimu wa Mulungu udaloŵa mwa ine nundiimiritsa, ndipo ndidamva Mulungu akulankhula. Adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, ndikukutuma kwa Israele, mtundu wa anthu aupandu amene andipandukira. Iwowo ndi makolo ao akhala akundichimwira mpaka lero lino. Anthu ake ndi okanika ndiponso achipongwe. Ndikukutuma kuti ukanene zimene Ine Ambuye Chauta ndikuŵauza. Ndiye popeza kuti iwowo ngaupandu, kaya akamvera kaya akakana, (pakuti ndi anthu opanduka) koma adzadziŵa ndithu kuti mneneri wafikadi pakati pao. Tsono iwe mwana wa munthu, usachite nawo mantha ndipo usaope zimene azikanena. Usachite mantha ngakhale minga ndi mkandankhuku zikuzinge ndipo ukukhala pakati pa zinkhanira. Komabe usaope mau ao ndipo usade nkhaŵa ndi mapenyedwe ao, chifukwa anthuwo ngaupandu. Popeza kuti iwowo ngaupandu, kaya akamvera kaya akakana, udzaŵauze ndithu mau anga. “Koma tsono iwe mwana wa munthu, umvere bwino zimene ndikukuuza. Usakhale waupandu ngati iwowo. Tsopano yasama, udye chimene ndikupatse.” Ine poyang'ana, ndidaona dzanja litaloza ine, litagwira mpukutu wolembedwa. Adaufunyulula nandiwonetsa. Mpukutu wonsewo unali wolembedwa kuseli nkuseri. Mau amene adaalembedwa m'menemo anali a za madandaulo, za maliro ndi za matemberero. Pamenepo Mulungu adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, idya chimene ndikukupatsachi. Idya mpukutuwu ndipo pita ukalankhule ndi Aisraele.” Motero ine ndidayasama, ndipo adandipatsa mpukutu kuti ndidye. Tsono adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, idya mpukutu ndikukupatsawu, ukhute.” Choncho ndidadya, ndipo unkatsekemera ngati uchi. Kenaka adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, pita kwa Aisraele, ukaŵauze mau anga. Sindikukutuma kwa anthu olankhula chilankhulo chachilendo ndi chovuta ai, ndikukutuma kwa Aisraele. Sindikukutuma kwa mitundu yambiri ya anthu amene chilankhulo chao nchachilendo ndi chovuta, amenenso sungathe kumvetsa zimene akulankhula. Ndithudi, ndikadakutuma kwa anthu achilendo otero, bwenzi iwo atakumvera. Koma Aisraele sadzakumvera, chifukwa safuna kundimvera Ine. Onsewo ngaliwuma ndi a mtima wosamvera. Tsono Ine ndidzakusandutsa waliwuma ndi wolimba mtima monga iwo omwewo. Ndidzakulimbitsa kupambana thanthwe lina lililonse, kuti ukhale wolimba ngati mwala wa daimondi. Usachite nawo mantha anthu aupanduwo.” Mulungu adapitiriza nati, “Iwe mwana wa munthu, umvetsetsetu zonse zimene ndikukuuza, ndipo uzikumbukire. Tsopano upite kwa Aisraele anzako amene ali ku ukapolo, ukalankhule nawo. Kaya akamvera kaya akakana, uzikaŵauza kuti, ‘Zimene akunena Ambuye Chauta nzakutizakuti,’ ” Pamenepo Mzimu wa Mulungu udandinyamula, ndipo kumbuyo kwanga ndidamva liwu lamphamvu ngati chivomezi chachikulu, lonena kuti, “Utamandike ulemerero wa Chauta kumene Iye amakhala!” Phokoso ndidaalimvalo linali la mapiko a zilengolengo zija akukhudzana mu mlengalenga, ndiponso phokoso la mikombero ya pambali pake ija, lomveka ngati chivomezi chachikulu. Mzimu wa Mulungu udandikweza ndi kundinyamula, ndipo ndidachokapo ndili ndi mtima woŵaŵa ndi wonyuka. Mphamvu za Chauta zidandiloŵa dzolimba. Motero ndidafika kwa amene anali ku ukapolo ku Telabibu, pafupi ndi mtsinje wa Kebara. Ndidakhala pansi pakati pao masiku asanu ndi aŵiri, ndili wothedwa nzeru kwabasi. Masiku asanu ndi aŵiriwo atatha, Chauta adandipatsira uthenga. Adati, “Iwe mwana wa munthu, ndakuika kuti ukhale mlonda woyang'anira Aisraele. Uzikati ukamva mau anga, uzikaŵachenjeza. Ndikauza munthu woipa kuti, ‘Munthu woipa iwe, udzafa,’ iwe nupanda kumchenjeza kuti aleke makhalidwe oipawo, kuti akhalebe ndi moyo, munthuyo adzafadi ali wochimwa, koma iweyo ndidzakuzenga mlandu chifukwa cha imfa yake. Koma munthu woipa ukamchenjeza kuti asiye njira zake zoipa, iye nkumapitirizabe makhalidwe ake oipawo, adzafa ali ochimwa, Koma iweyo udzapulumutsa moyo wako. “Ngati munthu wokhulupirira ayamba kuchita uchimo, Ine nkumuika m'zoopsa, ameneyo adzafa. Ngati iweyo sudamchenjeze, inde adzafa chifukwa cha kuchimwa kwakeko, ndipo kukhulupirika kwake sindidzakukumbukira, koma tsono mlandu wa imfa yake udzakhala pa iwe. Koma ukamchenjeza kuti asachimwe, iye nkulekadi kuchimwa, mosapeneka konse adzapulumutsa moyo wake, chifukwa chotsata chenjezo lako. Ndipo iwenso udzapulumutsa moyo wako.” Nthaŵi ina ndidamva kuti mphamvu za Chauta zandiloŵa kwambiri, ndipo Iye adandiwuza kuti “Nyamuka, upite ku chigwa. Ndidzalankhula nawe kumeneko.” Choncho ndidanyamuka kupita ku chigwa. Kumeneko ndidaona ulemerero wa Chauta, monga momwe ndidaauwonera ku mtsinje wa Kebara. Pomwepo ndidadzigwetsa pansi chafufumimba. Koma Mzimu wa Mulungu udaloŵa mwa ine, ndipo udandiimiritsa. Apo Chauta adandilankhula nandiwuza kuti, “Pita kwanu, ukadzitsekere m'nyumba mwako. Ndipo kumeneko, iwe mwana wa munthu, adzakumanga ndi zingwe, kotero kuti sudzatha kuyendanso pakati pa anthu. Ndidzakangamiza lilime lako kukhosi, kotero kuti sudzathanso kulankhula ndi kuŵachenjeza, chifukwa ndi anthu aupandu. Koma pamene ndidzayambe kulankhula nawe, ndidzakupatsa mphamvu zolankhulira. Ndipo udzaŵauze kuti, ‘Zimene akunena Ambuye Chauta nzakutizakuti.’ Wofuna kumva, amve. Wosafuna kumva, akhale, popeza kuti anthuwo ngaupandu.” Mulungu adati, “Iwe mwana wa munthu, tenga phale, uliike pamaso pako, ndipo ulembepo chithunzi cha mzinda wa Yerusalemu. Mzindawo uuzinge ndi ngalande, uunde mitumbira yankhondo, uuzinge ndi zithando zankhondo ndipo uzike makina ogumulira, kuzungulira mzindawo. Utenge chitsulo, uchiimike ngati khoma lachitsulo pakati pa iwe ndi mzindawo. Uyang'anitsitse mzindawo, ndipo uumangire zithando zankhondo ndi kuuzinga kotheratu. Chimenechi chidzakhala chizindikiro kwa Aisraele.” “Tsono ugonere kumanzere kwako, ndipo machimo a anthu a ku Israele ndidzaŵaika pa iwe. Udzasenza machimo aowo masiku onse amene udzagonere mbali imeneyo. Ndachitatu kukuikira masiku, okwanira 390, kulinganiza ndi zaka za machimo ao. Umu ndimo m'mene udzasenzere machimo a Aisraele. Utatha zimenezi, udzatembenuke nkugonera ku dzanja lamanja. Tsono udzasenze machimo a anthu a ku Yuda pa masiku makumi anai, tsiku lililonse kulinganiza ndi chaka chathunthu cha chilango chao. Uyang'anitsitse zithando zankhondo zozinga Yerusalemu. Ukwinye dzanja la mkanjo wako, ukweze mkono wako ndipo ulose modzudzula Yerusalemu. Ndithudi, ndidzakumanga ndi zingwe, kotero kuti sudzatha kutembenukira uku ndi uku, mpaka kuzingidwa kwa Yerusalemu kutatha. “Tsopano tenga tirigu ndi barele, nyemba ndi mphodza, mapira ndi mcheŵere, zonsezo uziike m'mbale imodzi, kenaka upange buledi. Uzidzadya pa masiku 390 amene udzakhale ukugonera mbali imodzi. Udzayeseko theka la kilogramu la bulediyo, kuti akhale chakudya chako. Uzidzadya kamodzi kokha pa tsiku. Uyesekonso makapu aŵiri a madzi, kuti akhale chakumwa chako cha tsiku ndi tsiku. Udzadya buledi wako wophika ngati makeke abarele. Ndoŵe youma ya anthu ndiyo idzakhale nkhuni zako zophikira, ndipo uzidzaphikira kumene anthu angathe kukuwona.” Tsono Chauta adati, “Buledi ameneyu ndiye chifaniziro cha chakudya chodetsedwa chimene Aisraele azidzadya ku maiko achilendo kumene ndidzaŵapirikitsire.” Koma ine ndidati “Inu Ambuye Chauta, inetu sindidadziipitsepo motero pa chipembedzo. Kuyambira ubwana wanga mpaka lero lino, sindidadyepo nyama yofa yokha kapena yojiwa ndi zilombo, ndipo sindidadyepo nyama yonyansa pa zachipembedzo.” Apo Iye adati, “Chabwino, ndidzakulola kuphikira ndoŵe ya ng'ombe m'malo mwa ndoŵe ya anthu, pophika buledi.” Kenaka adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, anthu a ku Yerusalemu ndidzaŵachepetsera buledi wa tsiku ndi tsiku. Anthuwo buledi wao azidzachita woyesa, ndipo azidzadya mwankhaŵa. Madzi aonso azidzachita oyesa, nkumamwa mwamantha. Motero chakudya ndi madzi zidzaŵathera pang'onopang'ono. Azidzada nkhaŵa akamapenyana, ndipo adzatheratu nkuwonda chifukwa cha machimo ao. “Iwe mwana wa munthu, tenga lupanga lakuthwa ngati lumo la wometa, umete tsitsi ndi ndevu. Tsono utenge choyesera, ugaŵe tsitsilo patatu. Kuzinga mzinda kuja kukatha, chimodzi cha zigawo zitatu za tsitsilo uchitenthe pakati pa mzinda. Chigawo chachiŵiri uchiduledule ndi lupanga, poyenda mozungulira mzinda wonsewo. Chigawo chachitatu uchimwazire ku mphepo, ndidzachitsata nditasolola lupanga. Utengeko tsitsi pang'ono, ulimange mu mpendero wa mkanjo wako. Pa tsitsi limeneli utapepo lina, uliponye pa moto, nkulitentha. Moto wa tsitsilo udzayaka mpaka kutentha Israele yense.” “Zimene akunena Ambuye Chauta ndi izi, akuti, ‘Uyu ndi Yerusalemu. Ndamuika pakati pa dziko lapansi, ndipo maiko onse akumzungulira. Koma anthu a ku Yerusalemu adapandukira malamulo anga, kupambana anthu a mitundu ina. Adakhala osamvera kupambana anthu a m'maiko ozungulira. Adakanadi malamulo anga ndipo sadasunge malangizo anga.’ Nchifukwa chake zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Chipongwe chanu nchachikulu kupambana cha anthu a mitundu yokuzungulirani. Simudatsate malamulo anga, simudasunge malangizo anga, koma mudatsata malamulo a anthu a mitundu yokuzungulirani. Nchifukwa chake Inenso ndakukanani. Ndidzakulangani anthu a mitundu ina akuwona. Ndidzakulangani ndi chilango chimene sindidakulange nachoni nkale lonse, ndipo sindidzakulanga nachoninso nkutsogolo komwe, poti zolakwa zanu nzonyansa kwambiri. Tsono mwa inu makolo adzadya ana ao ndipo ana adzadya makolo ao. Ndidzakulanganidi, ndipo onse otsala pakati pa inu, ndidzaŵamwazira ku mphepo zonse zinai.” “Pali Ine ndemwe Mulungu wamoyo, ndidzakuwonongani mopanda chifundo, chifukwa choti mwaipitsa Nyumba yanga ndi mafano anu oipa ndi miyambo yanu yonyansa. Tsono Ine sindidzakulekererani, sindidzakuchitirani chisoni mpang'ono pomwe. Chimodzi mwa zigawo zitatu za anthu anu chidzafa ndi mliri, kapena chidzaonongeka ndi njala. Chigawo china chidzaphedwa ndi lupanga kunja kwa mzinda. Ndipo chigawo china ndidzachimwazira ku mphepo zonse zinai, pochita kuchipirikitsa ndi lupanga langa losolola.” “Ndimo m'mene udzachitire mkwiyo wanga, ndipo ndidzaŵakalipira mpaka mtima wanga utakhala pansi. Choncho adzadziŵa kuti Ine Chauta ndidalankhula mwansanje pokulangani monga m'mene ndachitiramu.” “Iwe Yerusalemu, ndidzakusandutsa bwinja. Udzakhala chinthu chonyozeka m'maso mwa anthu a mitundu yokuzungulira ndi kwa onse odutsapo. Udzakhala chinthu chonyozeka, ndipo adzakunyodola. Udzakhala ngati chenjezo ndi chinthu choopsa kwa mitundu ya anthu okuzungulira, pamene ndidzakulanga mwamphamvu ndi kugamula mlandu wako mokwiya ndi mwaukali. Ndatero Ine Chauta. Ndidzakulasa ndi njala yolasa ngati mivi yoopsa ndi yosakaza, kuti ndikuwononge. Ndidzagwetsa njalayo pa iwe pochepetsa chakudya chako cha tsiku ndi tsiku. Ndidzatumiza njala ndi zilombo zakuthengo ndipo zidzakulanda ana ako. Ndidzakugwetsa ndi mliri ndipo padzakhala kuphana pakati pa anthu ako. Ndidzakudzetsera nkhondo yokuwononga. Ndatero Ine Chauta.” Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, uyang'ane ku mapiri a ku Israele, ndipo uŵadzudzule ndi mau aŵa akuti, Inu mapiri a ku Israele, imvani mau a Ambuye Chauta. Akuuza mapiri ndi magomo, mitsinje ndi zigwa kuti, ‘Ine weniweniyo ndidzakuthirani nkhondo, ndipo ndidzaononga akachisi anu opembedzerako mafano. Maguwa anu ansembe adzaonongedwa, ndipo maguwa anu ofukizirapo lubani adzaphwanyidwa. Anthu anu odzapembedza pamenepo ndidzaŵaphera pafupi ndi mafano anu. Tsono mitembo ya Aisraele ndidzaimwaza patsogolo pa mafano ao. Ndidzamwaza mafupa anu pozungulira maguwa anu onse. Konse kumene mukakhale, mizinda yanu idzasanduka mabwinja. Akachisi onse adzaonongedwa, kotero kuti maguwa anu onse pamodzi ndi mafano anu omwe adzaphwanyidwa. Maguwa anu ofukizirapo lubani adzagwetsedwa, ndipo zonse zimene mudapanga zidzatheratu. Anthu anu adzaphedwa pakati panu, motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.’ ” “Komabe ena mwa inu ndidzaŵasiya amoyo. Adzapulumuka ku nkhondo, ndipo ndidzaŵamwazira ku maiko ena, pakati pa anthu a mitundu ina. Tsono opulumuka mwa inu adzandikumbuka pakati pa anthu a mitundu inayo, kumene adatengedwa ukapolo. Ndidzaŵamvetsa chisoni ndi manyazi chifukwa cha kusakhulupirika kuja ndi kundipandukira kuja, ndiponso chifukwa cha kuika mtima kwao pa mafano. Tsono adzachita nyansi ndi iwo eniakewo poona zoipa zonse zimene adachita, pamodzi ndi zochita zao zonyansa. Pamenepo adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndipo sindinkaŵaopseza chabe pamene ndinkanena kuti ndidzaŵalanga.” “Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Omba m'manja mwako, ndipo uponde phazi lako pansi kwamphamvu. Tsono unene kuti, ‘Tsokalo!’ chifukwa cha zonyansa zonse zimene banja la Israele lachita. Adzafa ndi nkhondo, njala ndi mliri. Amene ali kutali adzafa ndi mliri. Amene ali pafupi adzafa ndi nkhondo. Aliyense wotsala adzafa ndi njala. Ndimo m'mene mkwiyo wanga udzagwere pa iwo. Apo mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, pamene mudzaona ophedwa ao ali vuu pakati pa mafano, kuzungulira maguwa ao, pamwamba pa magomo ndi mapiri onse, pansi pa mtengo uliwonse wogudira, ndi wa thundu uliwonse wa masamba ambiri, ku malo onse kumene ankapereka nsembe zonunkhira kwa mafano ao onse. Motero ndidzaŵakantha ndi mkono wanga, ndipo dziko lao lonse ndidzalisandutsa chipululu ku malo ao onse kumene akukhala. Ndidzalisandutsa bwinja kuchokera ku chipululu mpaka ku mzinda wa Ribula. Pamenepo adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.” Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, Ine Ambuye Chauta ndikuuza dziko la Israele kuti chimalizo chili pafupi. Chimalizo chafika ku mbali zonse zinai za dziko. Tsopano chimalizo chili pa iwe Israele. Mkwiyo wanga ndidzauthira pa iwe. Ndidzagamula mlandu wako potsata mayendedwe ako, ndipo ndidzakulanga chifukwa cha zonyansa zako. Sindidzakumvera chifundo kapena kukuleka. Ndidzakulanga chifukwa cha machitidwe ako ndiponso chifukwa cha zonyansa zimene zili pakati pako. Pamenepo udzadziŵa kuti Ine ndine Chauta. “Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Chiwonongeko chikubwera, chiwonongeko chotsatana nchinzake. Chimalizo chafika, chimalizo chija chafika! Chakugwera, ndithu chabwera. Inu anthu okhala m'dziko, chiwonongeko chanu chafika. Nthaŵi yafika, tsiku lili pafupi, tsiku lachisokonezo, osati lachimwemwe, ku mapiri. Posachedwapa ndidzakukwiyirani, ndipo ukali wanga udzathera pa inu. Ndidzagamula mlandu wanu potsata makhalidwe anu, ndipo ndidzakulangani chifukwa cha zonyansa zanu zochuluka. Sindidzakumverani chifundo kapena kukulekani ai. Ndidzakulangani potsata makhalidwe anu ndiponso chifukwa cha zonyansa zimene mumachita. Pamenepo mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, amene ndakulangani.” “Onanitu tsiku latsoka! Onanitu chikubwera! Chilango chanu chafika. Kunyada kwanu kwakakata, kudzitama kwanu kwaonekera poyera. Ndeu zasanduka chilango cha kuipa kwao. Palibe ndi mmodzi yemwe mwa iwo amene adzatsale. Zinthu zao zidzatha, chuma chao chidzathanso, ndipo ulemerero wao womwe udzatha.” “Nthaŵi yafika, tsiku layandikira. Wogula asakondwe, ndipo wogulitsa asamve chisoni, pakuti ukali wanga waŵagwera onse chimodzimodzi. Wogulitsa sadzazipezanso pa moyo wake wonse zimene adagulitsa kwa wina, pakuti chilango chidzagwera onsewo, sichingasinthike. Chifukwa cha machimo ake, palibe aliyense amene adzapulumutsa moyo wake. Lipenga lalira, ndipo onse akonzeka. Koma palibe ndi mmodzi yemwe amene akupita ku nkhondo, pakuti mkwiyo wanga wagwera onse pamodzi. “M'miseu akumenyana, m'nyumba muli mliri ndi njala. Anthu okhala ku midzi adzafa ndi nkhondo. Okhala m'mizinda adzafa ndi mliri ndi njala. Ngati otsala adzapulumukepo, azikakhala ku mapiri, nkumalira ngati nkhunda. Aliyense azidzabuula chifukwa cha tchimo lake. Manja onse adzalefuka, maondo adzangoti zii, kulobodoka ngati madzi. Adzavala ziguduli, ndipo adzagwidwa ndi mantha. Adzakhala ndi nkhope zamanyazi, kumutu adzameta mpala. Adzataya siliva wao m'miseu, ndipo golide wao adzamuwona ngati wonyansa. Siliva wao ndi golide wao sadzatha kuŵapulumutsa pa tsiku limene Chauta adzaonetse ukali wake. Chuma chaochi sichingaŵathandize kuthetsa njala, kapena kukhala okhuta, pakuti ndicho chidaŵagwetsa m'machimo.” “Kale ankanyada chifukwa cha zodzikongoletsera zao zamakaka. Koma ankazigwiritsa ntchito popanga mafano onyansa. Nchifukwa chake zodzikongoletsera zaozo ndidzazisandutsa zoŵanyansa. Ndidzazipereka kwa anthu akudza kuti azifunkhe. Anthu oipa kwambiri a pa dziko lapansi adzazilanda ndi kuziipitsa. Ine ndidzaŵalekerera anthuwo, kuti adzaipitse malo anga okondedwa. Adzaloŵamo ngati mbala nkuipitsamo. “Konzani maunyolo, popeza kuti anthu opha anzao achuluka m'dziko, mzinda wadzaza ndi ndeu. Ndidzatuma mitundu ya anthu yoipa kwambiri kuti ilande nyumba zao. Amphamvu pakati panu kunyada kwao kudzaŵathera, pamene ndidzalole mitundu yachilendoyo kuti iwononge malo amene amapembedzerapo. Pamene nkhaŵa idzaŵafikira, adzafunafuna mtendere, koma osaupeza. Tsoka lidzatsatana ndi tsoka linzake, padzakhala mphekesera zosatha. Anthu adzafunafuna mneneri kuti aŵalosere zakutsogolo, adzasoŵa ansembe oŵaphunzitsa malamulo, ndipo akuluakulu sadzakhalanso ndi uphungu. Mfumu idzalira, akalonga ake adzachita mantha. Manja a anthu am'dzikomo adzauma ndi mantha. Ndidzaŵalanga moyenerera machimo ao, ndidzaŵaweruza monga momwe iwowo adaŵeruzira anzao. Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.” Tsiku lachisanu la mwezi wachisanu ndi chimodzi, chaka chachisanu ndi chimodzi cha ukapolo, ndidaali khale m'nyumba mwanga pamodzi ndi akuluakulu a ku Yuda. Mwadzidzidzi mphamvu za Ambuye Chauta zidandifikira. Ine ndiyang'ane, ndidaona chinthu chooneka ngati munthu. Munthuyo kuchokera m'chiwunomu kumapita m'munsi anali ngati moto. Kuchokera m'chiwuno kukwera m'mwamba anali ngwee ngati mkuŵa wonyezimira. Adatambalitsa chinthu chonga dzanja nandigwira tsumba. Pomwepo mzimu wa Mulungu udandikweza mu mlengalenga. Ndipo ngati ndikuwona Mulungu kutulo, udapita nane ku Yerusalemu, nundiika pa khoma loloŵera ku chipata cham'kati choyang'ana kumpoto. Kumeneko kunali fano loputa mkwiyo wa Mulungu. Ulemerero wa Mulungu wa Israele udaoneka kumeneko, monga momwe ndidaaonera kale m'masomphenya m'chigwa muja. Pamenepo Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, tayang'ana kumpoto.” Ine nkuyang'anadi kumpoto. Kumeneko, pafupi ndi guwa pa khomo la chipata, ndidaona fano loputa mkwiyo wa Mulungu lija. Chauta adandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuwona zimene Aisraele akuchitazi, zonyansa zazikulu zimene akuchita kuno, zondichotsa ku Nyumba yanga yoyera? Ndipotu udzaona zonyansa zina zazikulu kuposa zimenezi.” Pambuyo pake adapita nane ku khomo loloŵera ku bwalo la Nyumba ya Mulungu. Ine poyang'ana, ndidaona dzenje pakhomapo. Tsono adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, boola pakhomapo.” Ndidabooladi, ndipo ndidapeza ngati khomo. Adandiwuza kuti, “Loŵa, uwone zonyansa zazikulu zimene anthu akuchita kuno.” Motero ndidaloŵa, ndipo pamakomapo ndidaonapo zithunzi za zinthu zosiyanasiyana zokwaŵa pansi, za nyama zonyansa ndiponso za mafano ena onse amene Aisraele ankapembedza. Atsogoleri a Aisraele makumi asanu ndi aŵiri anali ataima pamenepo. Yazaniya, mwana wa Safani, anali pakati pao. Aliyense mwa iwo anali ndi chofukizira lubani m'manja, ndipo utsi wa fungo lokoma la lubani unkatuluka m'menemo. Tsono Chauta adandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuwona zimene akulu a Israele akuchita mumdima muno? Aliyense akupembedza fano lakelake m'nyumbamu. Akunena kuti, ‘Chauta sakutiwona! Chauta walisiya dziko!’ ” Chauta adandiwuzanso kuti, “Udzaŵaonanso akuchita zonyansa zina zazikulu kupambana zimenezi.” Pambuyo pake adapita nane ku chipata cha ku Nyumba ya Chauta choyang'ana kumpoto. Kumeneko ndidaona akazi ena atakhala pansi, akulira mulungu wao wotchedwa Tamuzi. Chauta adati, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuziwona zimenezi? Komabe udzaona zonyansa zina zazikulu kupambana zimenezi.” Kenaka adapita nane ku bwalo lam'kati la Nyumba ya Chauta. Kumeneko, ku khomo loloŵera ku Nyumba ya Chauta, pakati pa khonde ndi guwa, kunali anthu aamuna ngati 25. Adaafulatira Nyumba ya Chautayo, nkhope zao zitaloza chakuvuma, ndipo ankapembedza dzuŵa choyang'ana kuvuma. Chauta adandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuziwona zimenezi? Ayuda sakukhutira nazo zonyansa akuchita panozi. Koma akufalitsanso zandeu m'dziko lonse. Motero akuutsa ukali wanga, akundipsetsa mtima ndi zochita zao. Tsono Ine ndidzaŵalanga ndili wokwiya. Sindidzaŵayang'ana ndi maso achifundo, ndipo sindidzaŵalekerera. Ngakhale adzalire mofuula kwa Ine, sindidzaŵamvera ai.” Pambuyo pake Chauta adandilankhulira m'makutu chokweza, adati, “Senderani pafupi, inu odzalanga mzindawu, aliyense akhale atatenga chida chake choonongera.” Pamenepo ndidaona anthu asanu ndi mmodzi akufika kuchokera ku chipata chakumtunda cha Nyumba ya Mulungu choyang'ana kumpoto chija, aliyense atatenga chida chankhondo. Pagulu paopo panali munthu wina wovala bafuta, atatenga zolembera pambalipa. Onsewo adaloŵa nakaima pambali pa guwa lamkuŵa. Tsono ulemerero woŵala wa Mulungu wa Israele udaoneka kuchokera mwa akerubi m'mene unaliri, nufika pa chiwundo cha Nyumba ya Mulungu. Chauta adaitana munthu wovala zabafuta uja amene anali ndi zolembera pambali pake. Adamuuza kuti, “Pita mu mzinda wonse wa Yerusalemu, ukaike chizindikiro pamphumi pa anthu onse amene akubuula ndi kulira chifukwa choipidwa ndi zonyansa zimene zikuchitika kumeneko.” Kenaka ndidamva Mulungu akuuza anzake ena aja kuti, “Mtsateni mumzinda monse, mukakanthe aliyense. Musakachite kaso ndi aliyense, musakachite konse chifundo. Muŵapheretu onse: okalamba, anyamata, atsikana, tiana, ndi akazi omwe. Koma musakhudze aliyense amene ali ndi chizindikiro chija. Muyambire ku Nyumba yanga yoyera.” Motero iwo aja adayambira kupha akulu a pakhomo pa Nyumba ya Chauta. Tsono Chauta adanena kuti, “Iipitseni Nyumba yangayo, ndipo mabwalo ake muŵadzaze ndi mitembo. Tiyeni, pitani!” Motero iwo adapita kukapha anthu mumzindamo. Pamene ankaŵapha, ine ndidatsala ndekha. Tsono ndidadzigwetsa pansi chafufumimba ndi kufuula kuti, “Aa! Inu Ambuye Chauta, kodi mwakwiya nawo ndithu anthu a ku Yerusalemu, kotero kuti mudzapha onse otsala ku Israele?” Mulungu adayankha kuti, “Uchimo wa Israele ndi Yuda ndi waukulu kwambiri. Dziko ladzaza ndi zophana, mzinda wadzaza ndi zosalungama. Anthu akunena kuti, ‘Chauta walisiya dzikoli. Sakuziwona zimene zikuchitikazi!’ Nchifukwa chake ine sindidzaŵamvera chifundo kapena kuŵalekerera. Ndidzaŵalanga potsata zochita zaozo.” Ndipo munthu wovala zabafuta uja, ali ndi zolembera pambali pake, adadzafotokozera Chauta kuti, “Ndachita zimene munandilamula zija.” Ndidayang'ana ku thambo lija lili pamwamba pa mitu ya akerubi, ndipo ndidaona chinthu chooneka ngati mpando waufumu wopangidwa ndi mwala wokoma wa safiro. Tsono Chauta adauza munthu wovala zabafuta uja kuti, “Pita pakati pa mikombero kunsi kwa akerubi, udzaze manja ako ndi makala oyaka amene ali pakati pa Akerubiwo. Tsono makalawo uŵawaze mu mzinda.” Ndipo ndidamuwona akupitadi. Ndiye kuti akerubi adaaimirira ku dzanja lamanja la Nyumba ya Chauta pamene munthuyo ankaloŵa. Ndipo mtambo udaadzaza bwalo lam'kati. Ulemerero woŵala wa Chauta udachoka pamene udaali, pamwamba pa akerubi, nukafika pa chiwundo cha Nyumba ya Mulungu. Tsono Nyumbayo idadzaza ndi mtambo uja, ndipo ulemerero woŵala uja wa Chauta udadzaza bwalo. Phokoso la mapiko a akerubi lidamveka mpaka ku bwalo lakunja, monga momwe limamvekera liwu la Mulungu Mphambe akamalankhula. Kenaka Mulungu adauza munthu wovala zabafuta uja kuti akapale moto pakati pa mikombero, kunsi kwa akerubi. Munthuyo adaloŵa nakaima pambali pa mkombero umodzi. Pomwepo mmodzi mwa akerubiwo adatambalitsa dzanja lake mpaka pa moto umene unali pakati pao. Adapalako motowo, napatsa munthu wovala zabafuta uja. Iyeyo adalandira motowo nkutuluka. Ndiye kuti kunsi kwa mapiko a akerubi kunali chinthu chooneka ngati dzanja lamunthu. Pambuyo pake ndidaona mikombero inai pambali pa akerubi. Pambali pa kerubi aliyense panali mkombero umodzi. Mikomberoyo inkanyezimira ngati miyala ya krizoliti. Maonekedwe a mikomberoyo anali ofanana, ndipo inali yoloŵanaloŵana. Poyenda akerubiwo ankapita mbali iliyonse mwa mbali zao zinai zimene ankayang'ana, osachita kutembenuka. Kumene mutu walunjika, nkumene ankapita. Matupi ao, misana yao, mapiko ao pamodzi ndi mikombero yonse inai, zonse zinali ndi maso. Ndidamva phokoso la mikombero monga lomwe ndidaalimva poyamba paja pamene ndinkaona zinthu m'masomphenya. Kerubi aliyense anali ndi nkhope zinai. Nkhope yoyamba inali ya kerubi, yachiŵiri inali ya munthu, yachitatu inali ya mkango, yachinai inali ya chiwombankhanga. Tsono akerubi aja adauluka. Akerubiwo anali zilengolengo zonzija zimene ndidaaona ku mtsinje wa Kebara. Akerubi ankati akamayenda, nayonso mikombero inkayenda m'mbali mwao. Pamene akerubi ankatambasula mapiko ao ndi kuuluka, mikombero inali m'mbali mwao ndithu. Zilengolengo zikaima, mikombero inkaimanso. Zikauluka, mikombero inkapita nawo ndithu, pakuti mzimu wa zilengolengozo ndiwo unkayendetsa mikomberoyo. Pamenepo ulemerero woŵala wa Chauta udachokapo pa chiwundo cha Nyumba yake nukakhalanso pamwamba pa akerubi. Apo Akerubi adatambasula mapiko ao nauluka. Ndidaŵaona akupita, mikombero ili pambali pao. Adakaima pa khomo lakuvuma la Nyumba ya Chauta. Ndipo ulemerero woŵala wa Mulungu wa Israele unali pamwamba pao. Zimenezi ndizo zilengolengo zimene ndidaaziwona ku mtsinje wa Kebara, kunsi kwa mpando waufumu wa Mulungu wa Israele. Ndidazindikira kuti zilengolengozo zinali akerubi. Akerubiwo aliyense anali ndi mapiko anai ndi nkhope zinai. Analinso ndi chinthu chooneka ngati dzanja lamunthu kunsi kwa mapiko ao. Nkhope zao zinali zonga zimene ndidaaziwona m'masomphenya ku mtsinje wa Kebara. Chilengolengo chilichonse chinkayenda molunjika kutsogolo. Mzimu wa Mulungu udandinyamula kupita nane ku chipata chakuvuma cha Nyumba ya Chauta. Poloŵerapo panali anthu 25, ndipo pakati pa anthuwo ndidaona atsogoleri aŵa a anthu: Yazaniya mwana wa Azuri, ndi Pelatiya mwana wa Benaya. Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, anthu aŵiri ameneŵa ndiwo amene amapangana zoipa nkumalangiza anthu zoipa mumzinda muno. Iwo amati, ‘Nthaŵi sinafike yoti nkumanga nyumba. Mzindawu uli ngati mphika umene uli pa moto, ifeyo tili ngati nyama imene ili mumphikamo.’ Tsono iwe mwana wa munthu, ulose moŵadzudzula, ulose ndithu.” Pamenepo Mzimu wa Chauta udandigwira, ndipo udandiwuza kuti, “Unene kuti zimene akunena Chauta ndi izi, akuti, ‘Inu a m'banja la Israele, ndikudziŵa zimene zili mumtima mwanu. Mwakhala mulikupha anthu ambiri mumzinda muno, ndipo mwaunjika mitembo yao m'miseu.’ “Nchifukwa chake Ambuye Chauta akunena kuti, ‘Mitembo ya anthu ophedwa imene mwaika kumeneko, imeneyo ndiyo nyama. Mzindawu ndiwo mphika ndithu. Koma ndidzakutulutsanimo. Mukuwopa lupanga, tsono ndidzakugwetserani lupangalo. Ndidzakutulutsani mumzimdamo, ndidzakuperekani kwa anthu akudza kuti akulangeni. Inunso mudzafa ndi lupanga, ndidzakulangani mpaka ku malire a Israele. Pamenepo mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta. Choncho mzindawo sudzakhalanso ngati mphika wokutetezani, ndipo simudzakhalanso ngati nyama yam'menemo ai. Ndidzakulangani mpaka ku malire a Israele. Pamenepo mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta. Simudatsate malangizo anga, simudamvere malamulo anga. Koma mwakhala mukutsata malamulo a mitundu ya anthu okuzungulirani.’ ” Pamene ndinkalosa, nthaŵi yomweyo Pelatiya mwana wa Benaya adafa. Tsono ndidadzigwetsa pansi chafufumimba nkufuula kuti, “Inu Ambuye Chauta, kodi mukufuna kuŵatheratu Aisraele onse otsala?” Pambuyo pake Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, achibale ako, ndiye kuti abale ako, anzako a ku ukapolo, onse a m'banja la Israele, anthu okhala ku Yerusalemu akuŵanena kuti, ‘Onse aja amene adatengedwa ukapolo ali kutali ndi Chauta, dziko lino tsopano nlathu.’ ” “Nchifukwa chake uza anzako a ku ukapolo kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ndine amene ndidaŵatumiza kutali pakati pa anthu a mitundu ina ndi kuŵabalalitsa ku maiko ambiri. Pakali pano ndikuŵasungabe kumaiko kumene adatengedwako.” “Nchifukwa chake unene ndithu kuti Ine Chauta mau anga ndikuti, Ndidzaŵasonkhanitsa kuchokera kwa anthu a mitundu inayo ndi kuŵasonkhanitsa pamodzi, kuchokera kumaiko kumene ndidaŵabalalitsa. Kenaka ndidzaŵapatsa dziko la Israele. Akadzaloŵa m'dzikomo, azidzachotsamo mafano onse oipa ndi onyansa. Ndidzaŵapatsa mtima watsopano, ndipo ndidzaika moyo watsopano mwa iwo. Ndidzachotsa mtima wouma ngati mwala mwa iwo, ndipo ndidzaŵapatsa mtima wofeŵa ngati mnofu. Motero adzatsata malamulo anga, adzasunga ndi kumvera malangizo anga. Choncho adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao. Koma amene mitima yao yazama m'zonyansa ndi zoipa zinazo, ndidzaŵalanga chifukwa cha zonse zimene adachita. Ndikutero Ine Chauta.” Tsono akerubi aja adayamba kuuluka, mikombero ili m'mbali mwao, ndipo ulemerero woŵala wa Mulungu wa Israele unali pamwamba pa iwo. Ulemerero wa Chautawo udakwera ndi kusiya mzindawo, nukaima pa phiri chakuvuma kwake kwa mzindawo. Pambuyo pake Mzimu wa Mulungu udandinyamula nukandifikitsa kwa akapolo ku dziko la Babiloni. Zonsezi zidachitika m'masomphenya, monga momwe Mzimu wa Mulungu udaandiwonetsera. Kenaka zinthu zimene ndinkaziwonazo zidayamba kuzimirira. Ndipo ndidaŵasimbira akapolo zonse zimene Chauta adaandiwonetsa. Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, ukukhala pakati pa anthu aupandu. Iwowo maso openyera ali nawo, komabe saona. Makutu omvera ali nawo, komabe saamva, chifukwa choti ngaupandu. Tsono iwe mwana wa munthu, longedza katundu wako wopita naye ku ukapolo. Ndipo unyamuke ulendo wako masana ndithu, iwo akuwona, ukachite ngati wopita ku ukapolo kuchoka kwanu kupita ku chilendo, iwowo akuwona. Mwina mwake iwo nkumvetsa ngakhale ali aupandu. Katundu wako wopita naye ku ukapolo umtulutse masana, iwo akuwona. Ndipo madzulo, iwo akuwona ndithu, uchoke kumudzi kwanu, monga ngati ukupita ku ukapolo. Uboole dzenje pa khoma, iwo akuwona, ndipo utulukire pamenepo. Usenze katundu wako pa phewa, iwo akuwona, ndipo upite kunja ku mdima. Uphimbe kumaso kotero kuti sungathe kuwona pansi, chifukwa ndakusandutsa chizindikiro chochenjeza anthu a m'banja la Israele.” Ndidachita monga momwe adandiwuzira. Ndidatulutsa katundu wanga masana, nditammanga ngati wopita naye ku ukapolo. Madzulo ndidaboola khoma ndi manja. Pamene chisisira chinkayamba, ndidasenza katundu wanga pa phewa kutuluka naye, iwo akuwona. M'maŵa mwake Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi Aisraele, anthu aupandu aja, suja adakufunsa kuti, ‘Ukuchita chiyani?’ Uŵauze kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Uthengawu ukunena za kalonga wa ku Yerusalemu ndiponso za banja lonse la Aisraele onse okhala kumeneko. Uŵauze kuti iwe ndiwe chizindikiro choŵachenjeza. Zimene zakuchitikira iwe, zidzaŵachitikiranso iwowo. Adzatengedwa kupita ku ukapolo. Kalonga wao adzasenza katundu wake nchisisira ndi kunyamuka. Adzatulukira pa dzenje limene anthu adaboola pa khoma, ataphimba kumaso kwake kuti asaone kumene akupita. Koma ndidzayala ukonde pa iye ndi kumkola mu msampha wanga. Ndidzapita naye ku Babiloni, ku dziko la Akaldeya, komabe iye sadzalipenya, ndipo adzafera kumeneko. Onse okhala naye pafupi, athandizi ake ndiponso ankhondo ake omwe, ndidzaŵabalalitsa ku mbali zonse zinai za dziko lapansi. Ndidzaŵalondola ndi lupanga losolola. Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndikadzaŵamwaza pakati pa mitundu yachilendo ndi kuŵabalalitsa ku maiko ambiri. Koma ndidzasiyako oŵerengeka amene adzapulumuke ku nkhondo, njala, ndi mliri, kuti akafotokoze nkhani yonse ya zochita zao zonyansa pakati pa mitundu ya anthu kumene akupitako. Apo adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.” Pambuyo pake Chauta adandipatsiranso uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, ukamadya, uzinjenjemera. Ukamamwa, uzinthunthumira ndi mantha. Anthu am'dzikomo uŵauze kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta za anthu okhala ku Yerusalemu ndiponso m'dziko la Israele ndi izi: Anthuwo adzadya buledi mwamantha ndi kumwa madzi mwankhaŵa. Dziko lidzafunkhidwa kwathunthu chifukwa cha nkhondo za anthu onse okhala m'menemo. Mizinda imene ili ndi anthu idzasakazika, ndipo dziko lidzasanduka chipululu. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.” Mau a Chauta adandifika akuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi mwambi umene ukumveka m'dziko la Israelewu ukutanthauza chiyani? Mwambiwo ukuti, ‘Masiku akuchuluka, komabe zolosa sizikuchitika.’ Tsono uŵauze anthu kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndiwuthetsa mwambi umenewu, sudzamvekanso ku Israele. Koma nthaŵi ili pafupi yoti zonse zimene ndidakuululirani m'masomphenya zidzachitikedi. Nthaŵi imeneyo sikudzakhalanso zinthu zina zonama zoziwona ngati kutulo. Sikudzakhalanso kuwombeza koshashalika pakati pa Aisraele. Ine Chauta ndidzanena zimene ndidzafune, ndipo zidzachitikadi. Sipakhalanso zochedwa ai, koma masiku anu omwe ano, Ine ndidzalankhula kwa inu anthu aupandunu, ndipo ndidzazichitadi,” ndikutero Ine Ambuye Chauta. Chauta adandipatsiranso uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, Aisraele akunena kuti zinthu zimene ukuziwona tsopano m'masomphenyazi sizidzachitika konse pa zaka zambiri. Akuti ukulosa zinthu za kutsogolo kwambiri. Tsono uŵauze kuti, Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Zonena zanga sizidzachedwanso ai. Ndidzachitadi chilichonse chimene ndanena. Ndikutero Ine Chauta!” Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, ulose zodzudzula aneneri a ku Israele. Amene amalosa za kukhosi kwao, zongopeka okha, uŵauze kuti amve mau a Ine Chauta! Ine Ambuye Chauta ndikunena kuti, Tsoka kwa aneneri opusa amene amachita kupeka zolosa zao, chonsecho sadaone chilichonse chochokera kwa Ine. Inu Aisraele, aneneri anu akhala ngati nkhandwe zam'mabwinja. Simudakwere khoma kuti mukakonze m'mene mudagumuka, kuti banja la Israele lidziteteze kolimba pa nkhondo, pa tsiku la Chauta. Aneneriwo amalankhula zonama, ndipo amalosa zabodza. Amanena kuti, ‘Akuterotu Chauta,’ pamene Chauta sadaŵatume konse. Komabe amayembekeza kuti zimene anenazo zidzachitika. Koma Ine ndikuti, Zimene inu aneneri mukuti mudaziwona m'masomphenya nzabodza. Ndipo kulosa kwanuko nkwabodza. Mumanena kuti ‘Akuterotu Chauta,’ ngakhale Ine sindidalankhule konse.” “Tsono zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ndikukutsutsani chifukwa choti mau anu ngachabe, ndipo zimene mukuti mudaziwona ngati kutulo nzabodza. Ndidzakantha aneneri onama amene amati adaona zakutizakuti ngati kutulo, amenenso kulosa kwao nkwabodza. Sadzakhala nao m'bwalo la aphungu la anthu anga. Sadzalembedwa m'kaundula wa nzika za Israele, ndipo sadzaloŵa m'dziko la Israele. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Ambuye Chauta. “Ndithudi aneneri asokeza anthu anga pomanena kuti, ‘Kudzakhala mtendere,’ pamene kulibe mtendere, ndipo chifukwa anthu akamanga khoma, aneneri amalipaka njereza. Uŵauze opaka njerezawo kuti khomalo lidzagwa. Mvula idzavumba mwamphamvu, kudzagwa matalala akuluakulu, ndipo kudzaomba mphepo yamkuntho. Pamenepo khomalo litagwa, nanga anthu sadzakufunsani kuti, ‘Kodi njereza imene mudapaka ija ili kuti tsopano?’ Nchifukwa chake zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ndidzakunthitsa mphepo yolimba nditakwiya. Ndidzavumbitsa mvula yamphamvu ndili ndi ukali. Ndidzagwetsa matalala akuluakulu mwachipseramtima, mpaka khomalo litaonongeka kotheratu. Ndidzagwetsa khoma limene mudalipaka njerezalo. Ndidzaligamuliratu mpaka maziko ake ataoneka. Pamene lidzagwa, inunso mudzafera momwemo. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta. Ndimo m'mene ndidzagwiritsire ntchito mkwiyo wanga pa khomalo ndi pa amene ankalipaka njereza aja. Apo ndidzakuuzani kuti, ‘Khoma lagwa, amene ankalimata aja nawonso agwera kumodzi. Agwanso aneneri a ku Israele amene ankalosa ku Yerusalemu, amene ankati adaona zamtendere m'masomphenya, pamene mtendere kunalibe.’ Ndikutero Ine Ambuye Chauta.” “Tsono iwe mwana wa munthu, ugwepo pa nkhani ya akazi amene ali pakati pa anthu ako. Iwowo amalosa zopeka za mumtima mwao, tsono uŵadzudzule. Uŵauze kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Tsoka kwa akazi amene amasoka zithumwa zapamkono, amenenso amasoka nsalu zakumutu za anthu a misinkhu yosiyanasiyana, kuti azikola mitima ya anthu. Kodi mufuna kukola mitima ya anthu anga, inuyo nkupulumutsa moyo wanu? Mwandichotsa ulemu pamaso pa anthu anga, chifukwa chofuna kulandira manja angapo a barele ndiponso zidutswa chabe za buledi. Mukupha anthu osayenera kufa, ndipo mukupulumutsa anthu osayenera kukhala moyo, pomanamiza anthu angaŵa amene amamva zabodza zanuzo. “Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikunena kuti, Ndikuzikana zithumwa zanu zapamkono, zimene mumakolera mitima ya anthu ngati mukukola mbalame. Ndidzazithothola pa mikono yanu, kuti ndiŵapulumutse anthuwo amene mumaŵakola ngati mbalame. Ndidzang'ambanso nsalu zanu zamankhwala zakumutu, ndipo ndidzapulumutsa anthu anga m'manja mwanu. Simudzakhalanso ndi mphamvu zoŵakolera. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta. Ndi mabodza anu mudatayitsa mtima anthu anga abwino amene Ine sindidafune kuti ataye mtima. Mudalimbitsa mtima anthu oipa kuti asaleke machimo ao, choncho satha kupulumutsa moyo wao. Nchifukwa chake zolosa zanu zabodza zimene mukuti mudaziwona ngati kutulo, simudzaziwonanso, ndipo simudzaombezanso. Ndidzapulumutsa anthu anga m'manja mwanu. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.” Tsiku lina akuluakulu ena a Aisraele adadza kwa ine nadzakhala pansi pamaso panga. Tsono Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, anthu ameneŵa aika mtima pa mafano ao, aikanso maso ao pa zinthu zina zophunthwitsa. Kodi iwoŵa akuganiza kuti ndidzaŵayankha akadzapempha nzeru kwa Ine? Tsono uŵauze kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ngati Mwisraele wina aliyense aika mtima pa mafano ake, naikanso maso ake pa zinthu zina zophunthwitsa, kenaka nkupita kwa mneneri, Ineyo Chauta mwiniwakene ndidzamuyankha moyenerana ndi kuchuluka kwa mafano ake. Ndidzatero kuti mwina mwake nkukopanso mitima ya Aisraele amene andisiya chifukwa cha mafano ao. “Nchifukwa chake uŵauze Aisraele kuti Ineyo Ambuye Chauta ndikunena kuti, ‘Lapani, mulekane nawo mafano anu. Muzisiye zonyansa zanu zonse.’ Ngati munthu wina aliyense, Mwisraele kapena mlendo wongokhala nao, andikana Ine, naika mtima pa mafano ake, ndi kuika maso ake pa zinthu zina zophunthwitsa, munthu woteroyo akabwera kudzapempha nzeru kwa Ine, kudzera mwa mneneri, Ine Chauta mwiniwakene ndidzamuyankha. Ndiye kuti ndidzalimbana naye munthu ameneyo. Ndidzamusandutsa chitsanzo ndi chisudzo, ndipo ndidzamchotsa pakati pa anthu anga. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta. “Ngati mneneri anyengedwa nalosa, ndine Chauta amene ndamnyenga. Ndipo ndidzamkantha ndi dzanja langa ndi kumchotsa pakati pa anthu anga Aisraele. Chilango cha mneneriyo ndi cha munthu amene adadzapempha nzeru kwa iyeyo, chidzalingana. Ndidzachita zimenezi kuti Aisraele asandithaŵenso, ndipo kuti asiye machimo ao. Pamenepo adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.” Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, dziko likandichimwira, posandikhulupirira Ine, ndidzalikantha ndi dzanja langa ndi kuchepetsa chakudya chake. Ndidzatumiza njala m'dzikomo, ndipo ndidzaononga anthu pamodzi ndi nyama zomwe. Ngakhale anthu atatu aŵa, Nowa, Daniele ndi Yobe, akadakhala kumeneko, akadangopulumutsa moyo wao wokha chifukwa cha kukhulupirika kwao. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.” Mwina ndikadatumiza zilombo kuti ziyende m'dzikomo ndi kuwononga anthu ake, mpaka dzikolo kusanduka chipululu chakuti munthu sangadutsemo chifukwa cha zilombo. Apo ngakhale anthu atatu aja akadakhala kumeneko, ndithu pali Ine ndemwe Ambuye Chauta amoyo, iwo aja sakadatha kupulumutsa ngakhale ana ao omwe. Akadangopulumutsa moyo wao wokha, koma dzikolo likadasanduka chipululu ndithu. “Mwina ndikadatumiza nkhondo ku dziko limenelo ndi kulamula kuti ipite m'dzikomo ndi kuwononga anthu ndi nyama zomwe. Apo ngakhale anthu atatu aja akadakhala kumeneko, ndithu pali Ine ndemwe Ambuye Chauta amoyo, iwo aja sakadapulumutsa ngakhale ana ao, akadangodzipulumutsa iwo okha. “Mwina ndikadatumiza mliri m'dziko limenelo, ndi kuwonetsa ukali wanga pokhetsa magazi ndi kuwononga anthu ndi nyama zomwe. Apo ngakhale Nowa, Daniele ndi Yobe akadakhala kumeneko, ndithu pali Ine ndemwe Ambuye Chauta amoyo, iwo aja akadadzipulumutsa iwo okha chifukwa cha kulungama kwao, koma ana ao ai. “Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Kudzakhala zoopsa kwambiri pamene ndidzagwetsa pa Yerusalemu zilango zanga zinai izi: nkhondo, njala, zilombo ndi mliri, kuti ziwononge anthu ndi nyama. Koma ena adzatsalako m'dzikomo odzatulutsa ana aamuna ndi aakazi, muŵapenyetsetse akadza kwa inu, muwone m'mene akhalire ndi zimene achite. Mitima yanu idzakhazikika pansi, mukakumbukira zoipa zimene ndachita ku Yerusalemu, chilango chonse chimene ndalanga nacho mzindawo. Mitima yanu idzakhaladi pansi, poona m'mene iwo akhalira ndi zimene akuchita, ndipo mudzamvetsa kuti Yerusalemu sindidamchite zimenezi popanda chifukwa. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.” Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi mtengo wamphesa umapambana bwanji wina uliwonse? Nthambi zake zimapambana bwanji nthambi za mitengo ina yakunkhalango? Kodi mtengo umene uja nkupangira chiyani? Kodi anthu angathe kupangira chokolekapo zinthu zao? Ha! Paja ndi nkhuni zosonkhera moto. Tsono moto utapsereza nsonga zake za mtengowo pamodzi ndi mphindikati yake, kodi nkugwira nawonso ntchito ina iliyonse? Ngakhale usanapse, sikukadatheka kugwira nawo ntchito. Nanga nanji utapserera ndi moto, adzaugwiritsa ntchito bwanji? “Nchifukwa chake zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Mtengo wamphesa ndidzauponya m'moto monga momwe ndimachitira mitengo ina yakunkhalango. Momwemonso ndi m'mene ndidzaŵachitire anthu a ku Yerusalemu, ndidzaŵalanga. Ngakhale athaŵe moto, motowo udzaŵatenthabe. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndikadzaŵalanga. Ndipo dziko laolo ndidzalisandutsa chipululu, chifukwa chakuti iwowo sadakhulupirike. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.” Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, umuwonetse Yerusalemu makhalidwe ake onyansa. Umuuze kuti, Ambuye Chauta akukuuza kuti, ‘Kanani ndi dziko la makolo ako, ndipo udabadwira kumeneko. Atate ako anali Mwamori, amai ako anali Muhiti. Ndipo utabadwa adakuchita izi: sadadule ntchofu yako, sadakusambitse m'madzi kuti akuyeretse. Sadakuthire mchere monga kudayenera, ndipo sadakukulunge m'nsalu. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adakusamala kapena kukumvera chisoni chokwanira kuti akuchitire zimenezi. Koma adakutaya panja poyera, chifukwa adaanyansidwa nawe pa tsiku limene udabadwa. “ ‘Ndiye Ine nditabwera, ndidakuwona ukuvimvinizika m'magazi ako. Ndidalankhula nawe uli m'magazi momwemo ndi kukuuza kuti, “Ukhale ndi moyo, ndipo ukule ngati mbeu ya m'munda.” Udakuladi, ndipo udatalika nkutha msinkhu. Maŵere adayamba kumera, tsitsi lako lidayamba kutalika. Komabe unali wamaliseche ndi wausiŵa. “ ‘Nditabweranso, ndidaona kuti nthaŵi yako yomanga banja idakwana. Tsono ndidakufunditsa mwinjiro wanga ndi kubisa maliseche ako. Ndidachita nawe chipangano chaukwati, ndipo udasanduka wanga. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. “ ‘Tsono ndidakusambitsa m'madzi ndi kukutsuka magazi ako, ndipo ndidakudzoza mafuta. Ndidakuveka zovala zopetapeta ndi nsapato zachikopa. Ndidakupatsa nsalu zabafuta ndi kukuveka zovala zasilika. Ndidakukongoletsa ndi zamakaka, nkukuveka zigwinjiri m'manja, ndi mkanda m'khosi mwako. Ndidakuveka chipini pa mphuno. Ndidakuika nsapule ku makutu ndi chisoti chaufumu chokongola kumutu kwako. Motero udavaladi zokongoletsa zagolide ndi zasiliva. Zovala zako zinali za bafuta wosalala, zasilika ndi za nsalu zopetapeta. Unkadya ufa wosalala, uchi ndi mafuta a olivi. Udakula mokongola zedi, ndipo udasanduka mfumukazi. Mbiri ya kukongola kwako idawanda pa dziko lonse lapansi, chifukwa choti ulemerero umene ndidakuveka nawo udakukongoletsa kwambiri. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. “ ‘Koma udadzitama nako kukongola kwako ndi kutchuka kwako, ndipo udayamba kuchita zadama. Unkachita chigololo, kumangodzipereka kwa aliyense amene wabwera. Udatengako zovala zako zina nukakongoletsera akachisi akoako, ndipo kumeneko unkakachitirako zigololo. Zotere sizinachitikepo, ndipo sizidzachitikanso. Udatenganso zokongoletsera, zopangidwa ndi golide wanga ndi siliva wanga, zimene ndidakupatsa, ndipo udapangira mafano achimuna amene udachita nawo chigololo. Mafanowo udaŵaveka zovala zako zopetapeta, ndipo udapereka mafuta anga ndi lubani wanga kwa iwo. Udatenga chakudya chimene ndidakupatsa, ufa, mafuta ndi uchi zimene ndinkakudyetsa, nuzipereka kwa iwo ngati nsembe za fungo lokoma. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. “ ‘Udatenga ana ako aamuna ndi aakazi amene udabalira Ine, nukaŵapereka ngati nsembe kwa mafano. Kodi zigololo zakozo sizidakukwanire, apa ukupha ana anga ndi kuŵapereka kwa mafano ako? Chifukwa cha zigololo zako zonyansazo, udaiŵala masiku a ubwana wako, pamene unali wamaliseche, wausiŵa ndi womangovimvinizika m'magazi ako.’ ” Ambuye Chauta akuti, “Uli ndi tsoka, ndithu uli ndi tsoka, chifukwa kuwonjezera pa zoipa zako zonsezo, udadzimangira nsanja pamodzi ndi guwa lake pa bwalo lililonse. Udamanga nsanja zakozo pa mseu uliwonse. Pamenepo udanyazitsa kukongola kwako, podzipereka kwa aliyense wodutsapo. Wakhala ukuchita zigololo kosaŵerengeka. Udachita zigololo ndi Aejipito adama oyandikana nawe, ndipo udandikwiyitsa chifukwa udachulukitsa zigololo zako. Ndidakukantha ndi dzanja langa ndipo ndidakuchepetserako dziko lako. Ndidakupereka kwa adani ako, Afilisti, amene ankaipidwa ndi makhalidwe ako onyansa. Chifukwa cha zilakolako zako udachitanso chigololo ndi Aasiriya. Pambuyo pake udapitirira kuchita chigololo ndi Ababiloni, anthu a m'dziko lokonda lamalonda. Komabe sudakhutire nazo.” Ambuye Chauta akunena kuti, “Mtima wako ndi wofooka kwambiri chifukwa udachita zonsezo monga ngati mkazi wadama wopanda manyazi. Udamanga nsanja ndi guwa lake pa mseu uliwonse ndiponso kachisi pa bwalo lililonse. Koma iweyo sunkachita monga amachitira adama ena, chifukwa sunkachitira malipiro. Mkazi wadama iwe, unkakonda amuna achilendo kupambana mwamuna wako. Amuna amapereka ndalama kwa akazi onse adama. Koma iwe zibwenzi zako zonse unkazipatsa mphatso. Potero unkazinyengerera kuti zizibwera kuchokera mbali zonse kudzagona nawe. Choncho udaali wosiyana ndi akazi ena pochita zadama, chifukwa panalibe amene ankakunyengerera kuti uchite naye chigololo. Iweyo ndiye amene unkapereka ndalama, osati ena kukupatsa ndalama ai. Motero unalidi wosiyana kwambiri ndi akazi ena.” “Tsono mkazi wadama iwe, imva mau a Chauta. Ambuye Chautawo mau ao ndi aŵa, Udavula mopanda manyazi, udaonetsa maliseche ako pochita zadama ndi zibwenzi zako ndi mafano ako, ndipo udapereka ana ako kuti aphedwe ngati nsembe zopereka kwa mafanowo. Nchifukwa chake ndidzasonkhanitsa abwenzi ako amene unkasangalala nawo, ndiponso onse amene unkaŵakonda pamodzi ndi onse amene unkadana nawo. Ndidzaŵasonkhanitsa kuchokera ku mbali zonse, nkukuvula pamaso pao, kuti iwowo adzaone thupi lako lonse lamaliseche. Ndidzakulanga monga amalangira akazi achigololo ndiponso opha anthu. Chifukwa cha nsanje yanga ndidzakhetsa magazi ako mokwiya kwambiri. Ndidzakupereka m'manja mwa abwenzi ako. Adzaononga nsanja zako ndi maguwa ako ndi kugwetsa akachisi ako aja. Adzakuvula zovala zako ndi kukukolopola zodzikongoletsera zako zabwinozo. Motero adzakusiya wamaliseche ndi wausiŵa. Adzatuma gulu la anthu kuti akuponye miyala ndi kukudula pafupipafupi ndi malupanga ao. Adzatentha nyumba zako, ndipo adzakulanga poyera, akazi ambiri akuwona. Ndidzathetsa dama lako, ndipo sudzazilipiranso zibwenzi zako. Pamenepo ndidzaleka, ukali wanga udzatha, ndipo sindidzakuchitiranso nsanje. Ndidzakhala phee, osachitanso ukali. Iwe udaiŵala masiku a ubwana wako, ndipo udandikwiyitsa ndi zinthu zonse zimene udachita. Nchifukwa chake Ine ndidzakubwezera pamutu pako chilango cha zimene udachitazo. Pajatu udaonjezera zigololo pa zonyansa zako zina zonse. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.” “Iwe Yerusalemu, akuluakulu adzakuphera mwambi uwu wakuti, ‘Mwana watengera cha make.’ Ndiwedi mwana wa mai wako amene adadana ndi mwamuna wake ndi ana ake. Ndiwe mbale wa abale ako amene adadana ndi amuna ao ndiponso ana ao. Mai wako anali Muhiti, bambo wako anali Mwamori. Mkulu wako ndi Samariya amene ankakhala cha kumpoto kwako pamodzi ndi midzi yake. Mng'ono wako amene ankakhala ndi midzi yake chakumwera kwako, ndi Sodomu. Iwe sudakhutire nkutsata njira zao zoipa ndiponso kuchita zonyansa. Koma patangopita nthaŵi pang'ono chabe, unkachita zoipa kupambana iwowo. Pali Ine ndemwe Chauta wamoyo, ngakhale mbale wako Sodomu ndi midzi yake sadachite monga m'mene iweyo wachitira pamodzi ndi midzi yako. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. Tchimo la mbale wako Sodomu linali lakuti iyeyo pamodzi ndi midzi yake ankanyadira chuma chake ndi chakudya chake chambiri, koma osalabadako zothandiza osauka ndi aumphaŵi. Ankadzitukumula kwambiri namachita zonyansa zambiri pamaso panga. Nchifukwa chake ndidaŵachotsa monga m'mene waoneramu. Ngakhale Samariya yemwe sadachite theka la machimo amene udachita iwe. Iweyo udachita zonyansa zambiri kupambana abale ako aŵiriwo, kotero kuti iwo amaoneka ngati osachimwa poyerekeza ndi iwe. Tsopano mwiniwakewe uyenera kuchita manyazi ndi kunyozedwa, iwe amene waonetsa abale ako ngati osachimwa. Machimo ako ndi onyansa kwambiri kupitirira a abale ako, motero iwo aoneka ngati osalakwa. Iwenso tsono, amene udaonetsa abale ako ngati osachimwa, uchite manyazi ndi kunyozedwa. “Koma ndidzadalitsanso Sodomu pamodzi ndi midzi yake. Ndidzachita chimodzimodzi ndi Samariya pamodzi ndi midzi yake. Pa nthaŵi yomweyo, nawenso Yerusalemu ndidzakudalitsa. Choncho uchite manyazi ndi kunyozedwa, chifukwa udaonetsa abale akoŵa ngati angwiro. Koma pamene mbale wako Sodomu pamodzi ndi midzi yake adzakhalanso monga momwe adaaliri kale, ndipo pamene mbale wako Samariya pamodzi ndi midzi yake adzakhalanso monga momwe adaaliri kale, nawenso ndi midzi yako udzakhalanso monga momwe udaaliri kale. Kodi kale lija pamene iwe unkanyada, paja unkakonda kujeda mbale wako Sodomu, kuipa kwako kusanadziŵike. Koma tsopano walingana naye posanduka chinthu chonyozeka kwa anthu a ku Edomu ndi kwa onse oyandikana nawo, ndiponso kwa Afilisti. Ndithu okuzungulira onsewo akukunyoza kwambiri. Motero iwe uyenera kulangidwa chifukwa cha zigololo zako ndi makhalidwe ako onyansa. Ndikutero Ine Chauta. “Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ndidzakulanga potsata zimene udachita. Iwe udanyoza lumbiro lako pakuphwanya chipangano. Komabe ndidzakumbukira chipangano chimene ndidachita nawe pa ubwana wako. Ndidzachita nawe chipangano china, chipangano chake chosatha. Tsono udzakumbukira makhalidwe ako akale. Udzachita manyazi pamene udzalandiranso abale ako, wamkulu ndi wamng'ono yemwe. Ndidzaŵapereka kwa iwe kuti akhale ngati ana ako aakazi, ngakhale kuti iwowo sali nao m'chipangano changa ndi iwe. Ndidzachita chipangano changa ndi iwe, ndipo udzadziŵa kuti Ine ndine Chauta. Ndikadzakukhululukira zoipa zako zonse zimene udachita, udzazikumbukira ndipo udzachita manyazi kwambiri, kotero kuti sudzathanso nkulankhula komwe. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.” Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, uŵaphere mwambi Aisraele ndi kuŵauza fanizo. Unene kuti Ambuye Chauta akuti, Panali chiwombankhanga chachikulu, cha mapiko akuluakulu, ndi nthenga zitalizitali za mathothomathotho. Chidadza ku Lebanoni. Chidagwira nthambi yapamwamba pa mtengo wa mkungudza, nkubudula nsonga yeniyeni ya nthambiyo. Chidapita nayo ku dziko lamalonda, nkukaiika mu mzinda wa anthu amalonda. Kenaka chidatenga mbeu ya m'dzikomo nkukaibzala pa malo achonde, pamene panali madzi ambiri pafupi. Chidaibzala monga momwe amabzalira mtengo wa msondodzi. Tsono idaphuka nisanduka mtengo wamphesa wotambalala cham'munsi. Nthambi zake zidaloza kumwamba kumene kunali chiwombankhangacho, koma mizu yake idazamira pansi. Choncho mtengo wamphesawo udasanduka wanthambi ndi wa masamba ambiri. “Koma panali chiwombankhanga chinanso chachikulu cha mapiko akuluakulu ndi cha nthenga zambiri. Mtengo wamphesa uja udapinda mizu yake kulozetsa kwa chiwombankhangacho. Ndipo udayang'anitsa nthambi zake kwa chimbalamecho, kuti mwina nkuzithirira madzi oposa amene anali m'mundamo. Koma mtengowo adaauwoka kale m'nthaka yachonde m'mene munali madzi ambiri, kuti uphuke nthambi ndi kubereka mphesa, ndi kukhala wokongola. “Ukanene kuti, Ambuye Chauta akuti, Kodi mtengo wamphesa umenewu udzakula bwino? Kodi chiwombankhanga chija sichidzauzula mizu ndi kubudula nthambi zake, kotero kuti masamba ake anthete adzafota? Nkosalira munthu wamphamvu kapena anthu ochuluka kuti auzuletu ai. Tsono ngakhale atauwoka pena, kodi udzakula bwino? Kodi sudzafota kotheratu ikadzaomba mphepo yakuvuma, kufotera pomwe auwokerapo?” Pamenepo Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Uŵafunse anthu aupanduŵa kuti, ‘Kodi mukulidziŵa tanthauzo lake la zimenezi?’ Uŵauze kuti mfumu ya ku Babiloni idaapita ku Yerusalemu, nikatengako mfumu ndi akalonga ake kupita nawo ku Babiloni. Idatenga mwana wina wa mfumu nkuchita naye chipangano, ndipo idamlumbiritsa kuti akhale womvera. Idachotsa akulu onse am'dzikomo, kuti ufumu wa dzikolo utsitsidwe, usadzatchukenso, koma kuti ukhalepobe pakungosunga chipangano chimene udachita. Koma mfumuyo idapandukira mfumu ya ku Babiloni, nitumiza akazembe ku Ejipito kukapempha akavalo ndi gulu lalikulu la ankhondo. Kodi mfumu yoteroyo ingapambane? Kodi ingathe kupulumuka ngati ichita zotero? Kodi ingathe kuphwanya chipangano, kenaka nkupulumuka?” “Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ndikulumbira pali Ine ndemwe wamoyo, kuti mfumuyo idzafera ku Babiloni, dziko lomwe la mfumu imene idamulonga ufumuyo. Idapeputsa lumbiro lake, nkuphwanya chipangano chimene idachita ndi mfumu inayo. Motero idzafera ku Babiloni. Farao pamodzi ndi gulu lake lankhondo adzalephera kuithandiza mfumuyo pamene ankhondo a ku Babiloni adzazinga mzinda wake ndi mitumbira yankhondo ndi nsanja zankhondo, kuti aononge anthu ambiri. Mfumu ya ku Yuda idanyoza lumbiro lake pakuphwanya chipangano. Idaalonjeza, komabe sidatsate malonjezowo. Choncho sidzapulumuka. “Tsono Ine Ambuye Chauta ndikuti, Pali Ine ndemwe wamoyo, iyeyo wapeputsa lumbiro lake limene adalumbira kwa Ine, ndipo waphwanya chipangano chimene ndidapangana naye. Motero ndidzamlanga chifukwa cha zoipa zake. Ndidzamtchera ukonde, ndipo ndidzamkola mu msampha wanga. Ndidzamtengera ku Babiloni, ndipo ndidzamlangira komweko, chifukwa choti sadakhulupirike kwa Ine. Asilikali ake onse amphamvu adzaphedwa ku nkhondo, ndipo opulumuka adzathaŵira ku mbali zonse. Motero mudzadziŵa kuti ndine Chauta amene ndanena zimenezi.” Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: “Ine ndemwe ndidzatenga kanthambi ka ku nsonga yapamwamba ya mtengo wa mkungudza, ndipo ndidzakabzala. Pa tinthambi tapamwamba ndidzathyolako kena kanthete ndipo ndidzakabzala pa phiri lalitali kwambiri. Ndidzakabzaladi pa phiri lalitali la ku Israele. Kadzaphuka ndi kubala zipatso zake. Motero kadzasanduka mkungudza wokoma. Mbalame za mitundu yonse zidzakhala mu mthunzi wa mtengowo. Mitengo yonse yam'dzikomo idzadziŵa kuti ndine Chautane amene ndimafupikitsa mitengo yaitali, ndiponso kutalikitsa mitengo yaifupi. Ndimaumitsa mitengo yobiriŵira, ndi kubiriŵiritsa mitengo youma. Ine Chauta ndanena zimenezi, ndipo ndidzazichitadi.” Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Chifukwa chiyani anthu a ku Israelenu mumakonda kubwerezabwereza mwambi uja wakuti, ‘Nkhuyu zodya akulu zidapota ndi ana omwe?’ Ndithu, pali ine ndemwe wamoyo, mwambi umenewu simudzaunenanso ku Israele. Moyo uliwonse ndi wanga. Moyo wa mwana ndi wanga, wa bambo ndi wanganso. Munthu amene wachimwa, ndiye amene adzafe. “Tiyese kuti pali munthu wabwino amene amatsata malamulo ndi kuchita zabwino. Iyeyo sadyera nao ku zitunda zachipembedzo. Sapembedza mafano a ku Israele. Saipitsa mkazi wa munthu wina. Sakhudza mkazi pamene ali wosamba. Sazunza munthu wina aliyense, koma amabwezera wangongole chigwiriro chake. Saaba, amadyetsa anjala, ndipo amaveka ausiwa. Sakongoza ndalama kuti apezepo phindu kapena kulandira chiwongoladzanja. Amadziletsa kuchita zoipa, ndipo sachita mokondera pogamula milandu ya anthu. Amatsata malangizo anga, ndipo amamvera malamulo anga mokhulupirika. Munthu wotereyu ndi wolungama, adzakhala ndi moyo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. “Mwina munthu wotero nkubala mwana amene ntchito yake nkuba ndiponso kupha anthu. Iye amachita zambiri zimene bambo wake sadachitepo. Amadyera nao ku zitunda zachipembedzo, amaipitsa mkazi wa munthu wina, amazunza osoŵa ndi osauka. Amaba, sabwezera chigwiriro cha munthu wangongole. Amatembenukira ku mafano, namachita zonyansa. Amakongoza kuti apezepo phindu, ndipo kuti alandire chiwongoladzanja. Kodi munthu wotereyu nkukhala ndi moyo? Ai ndithu, sadzakhala ndi moyo. Chifukwa adachita zoipa zonsezi, adzaphedwa, ndicho chilango chomuyenerera. “Mwina mwake munthu woipa uja nkubala mwana amene aona machimo a bambo wake. Amaona, koma satsanzirako. Sadyera nao ku zitunda zachipembedzo. Sapembedza mafano a ku Israele, saipitsa mkazi wa munthu wina, sazunza munthu wina aliyense, satenga chigwiriro ndipo saaba. Koma amadyetsa anjala ndi kuveka ausiŵa. Amakana kuchita zoipa, sakongoza kuti apezepo phindu kapena kuti alandire chiwongoladzanja. Amatsata malangizo anga ndi kumvera malamulo anga. Munthu woteroyo sadzafera zolakwa za bambo wake. Adzakhala ndi moyo. Koma bambo wake, popeza kuti adachimwa pozunza anthu ena ndi kubera mbale wake ndiponso kuŵachita zoipa anansi ake, adzafera zoipa zakezo. “Mwina mungathe kufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mwana salangidwa chifukwa cha zolakwa za bambo wake?’ Mwanayo adzakhala ndi moyo chifukwa choti nthaŵi zonse ankachita zolungama ndi zokhulupirika, ndipo ankamvera malamulo anga onse mosamala. Munthu wochimwa ndiye amene adzafe, osati wina. Mwana sadzafera machimo a bambo wake, ndipo bambo sadzafera machimo a mwana wake. Munthu wabwino adzakolola zipatso za ubwino wake. Munthu woipa adzakolola zipatso za kuipa kwake. “Munthu wochimwa akaleka machimo ake amene ankachita, namamvera malamulo anga onse, ndi kumachita zolungama ndi zokhulupirika, ndithudi ameneyo adzakhala ndi moyo, sadzafa. Zoipa zake zonse zidzakhululukidwa. Adzakhala ndi moyo chifukwa cha ntchito zake zolungama. Ine Ambuye Chauta ndikuti, Kodi imfa ya munthu woipa Ine ndimakondwera nayo? Iyai, koma ndikadakonda kuti woipa aleke njira zake zoipa ndi kukhala ndi moyo. “Koma munthu wabwino akasanduka woipa, namachita zonyansa za mitundu yonse zimene anthu amachita, kodi munthu woteroyo nkukhala ndi moyo? Iyai, ntchito zake zonse zabwino sizidzakumbukika. Wapalamula, wachimwa, adzafa basi. Koma inu mumati, ‘A! Zimene Ambuye amachitazi nzopanda chilungamo.’ Tamvani tsono Aisraele inu: Kani zochita zanga ndiye zosalungama? Kodi si zochita zanu zimene zili zosalungama? Ngati munthu wabwino aleka kuchita zoyenera, namachita zoipa, adzafa chifukwa cha zoipa zakezo. Komanso munthu woipa akaleka zoipa zake, namachita zoyenera, adzapulumutsa moyo wake. Poti adazindikira kuipa kwa zolakwa zake, nazileka, ndiye kuti adzakhala ndi moyo, sadzafa. Komabe Aisraele akunena kuti zochita za Ambuye nzosalungama. Pepani, Aisraele inu, ndinu amene mumachita zosalungama, osati Ine. “Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Aisraele inu, aliyense mwa inu ndidzamuweruza molingana ndi ntchito zake. Lapani, tembenukani mtima, kuti machimo anu asakuwonongeni. Tayani zoipa zanu zonse zakale zimene mudachimwira Ine. Mukhale ndi mtima watsopano ndi nzeru zatsopano. Nanga muferenji, inu anthu a ku Israele? Sindikondwera nayo imfa ya munthu wina aliyense. Nchifukwa chake lapani, kuti mukhale ndi moyo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.” Chauta adandiwuza kuti, “Tsono iwe, uimbe nyimbo yamadandaulo, kuimbira akalonga aŵiri aja a ku Yerusalemu. Mau ake unene kuti: “ ‘Mai wako anali ngati mkango waukazi pakati pa mikango yaimuna. Ankagona pakati pa mikango yaimuna akulera ana ake. Adalera mmodzi mwa ana ake, ndipo mwanayo adasanduka mkango. Udaphunzira kugwira nyama, nuyamba kudya anthu. Tsono mitundu ya anthu idachenjezana za mkangowo, ndipo tsiku lina udagwa m'mbuna yao. Adaukoka ndi ngoŵe kupita nawo ku dziko la Ejipito. Mai uja ataona kuti mwana ankamukhulupirirayu wagwidwa, adakuzanso wina mwa ana ake, namsandutsa mkango wamphamvu. Unkayendayenda pakati pa mikango inzake, pakuti unali mkango wokhwima. Udaphunzira kugwira nyama, nuyamba kudya anthu. Udagwetsa malinga ao, ndipo udaononga mizinda yao. Onse a m'dzikolo adachita mantha chifukwa cha phokoso la kubangula kwake. Tsono mitundu ya anthu, makamaka a m'maiko ozungulira, adabwera kudzalimbana nawo. Adautchera ukonde, ndipo udagweradi m'mbuna yao. Adaukoka ndi ngoŵe nauponya m'chitatanga. Adapita nawo kwa mfumu ya ku Babiloni, mfumuyo nkuuponya m'ndende. Choncho liwu lake silidamvekenso ku mapiri a ku Israele. “ ‘Mai wako anali ngati mpesa m'munda wa mphesa wobzalidwa m'mbali mwa madzi. Udabereka bwino ndipo unali ndi nthambi zambiri, chifukwa panali madzi ambiri. Unali ndi nthambi zolimba zoyenera kupangira ndodo zaufumu. Udatalika nusomphoka pakati pa zomera zina, ndipo unkaoneka bwino chifukwa cha kutalika kwake ndi kuchuluka kwa nthambi zake. Koma adauzula mwaukali naugwetsa pansi. Udauma ndi mphepo yakuvuma, zipatso zake zidayoyoka, thunthu lake lidauma, mtengo wonse nkupserera ndi moto. Tsono adauwokanso ku chipululu ku dziko louma, lopanda madzi. Ndipo moto udayaka mumtengomo, nupsereza nthambi ndi zipatso zake. Motero ulibenso nthambi yolimba yoti nkupangira ndodo ya mfumu.’ ” Imeneyi ndi nyimbo yachisoni, ndipo yasanduka nyimbo yapamaliro. Tsiku lakhumi la mwezi wachisanu, chaka chachisanu ndi chiŵiri cha ukapolo, akuluakulu ena a ku Israele adabwera kudzapempha nzeru kwa Chauta. Tsono adakhala pansi pamaso panga. Pamenepo Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, akuluakulu a ku Israele uŵauze mau anga akuti, Kodi mwabwera kudzapempha nzeru kwa Ine? Pali Ine ndemwe, sindilola zotere. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuvomera kudzaŵaweruza? Kodi udzagamula mlandu wao? Tsonotu uŵafotokozere zonyansa zonse zimene adachita makolo ao. Pambuyo pake uŵauze mau anga akuti, Pa tsiku limene ndidasankhula Israele, ndidalumbira kwa zidzukulu za Yakobe, ndipo ndidadziwulula kwa iwo ku Ejipito. Ndidalumbira ndi kuŵauza kuti, ‘Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.’ Tsiku limenelo ndidalumbira kwa iwo kuti ndidzaŵatulutsa m'dziko la Ejipito, kupita nawo ku dziko limene ndidaŵapatsa, dziko lamwanaalirenji, lokongola kwambiri kupambana maiko ena. Ndidaŵauza onse kuti aliyense ataye zonyansa zonse zimene ankasangalala nazo, ndipo asadziipitse ndi mafano a ku Ejipito. Ine ndine Chauta Mulungu wanu. Koma adandipandukira, adakana kundimvera. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adasiya zonyansa zake zimene ankasangalala nazo. Palibe amene adasiya mafano a ku Ejipito. Tsono ndidaganiza zoŵaonetsa ukali ndi mkwiyo wanga ku Ejipito komwe. Koma sindidachite zimenezo, kuti choncho dzina langa lilemekezeke, lisanyozeke pakati pa anthu a mitundu ina amene Aisraele ankakhala nawo. Paja ndinali nditaonetsa mphamvu zanga pamaso pa mitunduyo pakutulutsa Aisraele m'dziko la Ejipito. “Ndidaŵatulutsadi ku Ejipito ndi kuŵatsogolera m'chipululu. Ndidaŵapatsa malangizo anga kumeneko, ndi kuŵaphunzitsa malamulo anga, amene amakhalitsa moyo anthu oŵamvera. Ndidaŵapatsanso masiku a Sabata kuti akhale ngati chizindikiro pakati pa Ine ndi iwo, kuti adziŵe kuti Ine Chauta ndimaŵayeretsa. Koma Aisraele adandipandukira m'chipululumo. Sadatsate malangizo anga ndipo adakana malamulo anga, amene amakhalitsa moyo anthu oŵamvera. Anthuwo adaipitsa kotheratu masiku anga a Sabata. Motero Ine ndidaganiza zoŵalanga mwaukali m'chipululu momwemo ndi kuŵaononga kotheratu. Koma zimenezo sindidazichite, kuti choncho dzina langa lilemekezeke, lisanyozeke pakati pa anthu a mitundu ina amene adandiwona ndikutulutsa Aisraelewo ku Ejipito. Kuwonjezera pamenepo, ndidalumbira kwa iwo m'chipululu nditakweza dzanja, kuti sindidzaŵaloŵetsa m'dziko limene ndinali nditaŵapatsa, dziko lamwanaalirenji, lokoma kwambiri kupambana maiko ena onse. Paja adakana malangizo anga, sadamvere malamulo anga, ndipo adaipitsa masiku anga a Sabata. Mtima wao udakonda kutsata mafano ao. Komabe ndidaŵamvera chisoni ndipo sindidaŵaononge ndi kuŵatheratu m'chipululu. “Ndidalamula ana ao m'chipululu kuti asatsate malangizo a makolo ao, asamvere malamulo ao, kapena kudziipitsa ndi mafano ao. Ndidati, ‘Ine ndine Chauta Mulungu wanu. Muzitsata malamulo anga, ndi kumvera malangizo anga. Muzilemekeza masiku anga a Sabata ngati opatulika, kuti adzakhale ngati chizindikiro pakati pa Ine ndi inu. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta Mulungu wanu.’ “Koma ana ao nawonso adandipandukira. Sadatsate malangizo anga, sadamvere malamulo anga, amene amakhalitsa moyo anthu oŵamvera. Ndiponso adaipitsa masiku anga a Sabata. Tsono ndidaganiza zoŵalanga mokwiya ndi kuŵalipsira m'chipululu momwemo. Koma sindidachite zimenezo, kuti choncho dzina langa lilemekezeke, lisanyozeke pakati pa anthu a mitundu ina amene adandiwona ndikutulutsa Aisraelewo ku Ejipito. Ndidachita kulumbira m'chipululu nditakweza dzanja, kuti ndidzaŵabalalitsa pakati pa mitundu ya anthu ndi kuŵamwazira ku maiko akutali, chifukwa sadamvere malamulo anga, adakana malangizo anga, adaipitsa masiku anga a Sabata, ndipo adapembedza mafano a makolo ao. Kuwonjezera pamenepo ndidaŵapatsa malamulo amene sankaŵakomera, ndiponso malangizo amene sakadatha kupeza nawo moyo wabwino. Ndidaŵalekerera kuti adziipitse ndi zopereka zao, makamaka pakupereka ana ao achisamba ngati nsembe zootcha. Ndidatero kuti ndiŵadetse nkhaŵa, ndipo kuti adziŵe kuti Ine ndine Chauta. “Iwe mwana wa munthu, lankhula nawo tsono Aisraele, uŵauze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Makolo anu adandinyozanso poleka kundikhulupirira, pamene ndidaŵaloŵetsa m'dziko limene ndidaachita kulumbira kuti ndidzaŵapatsa. Kulikonse kumene adaona chitunda chachitali ndi mtengo wogudira, kumeneko ankapereka nsembe ndi zopereka zao zondikwiyitsa. Kumeneko ankapereka nsembe za fungo lokoma, ndiponso nsembe zazakumwa. Ndidaŵafunsa kuti, Kodi chitunda kumene mukupitako nchotani? Choncho dzina lake lakhala ‘Chitunda chachipembedzo’ mpaka lero.” “Tsono uŵauze Aisraele kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Kodi mudzadziipitsa monga momwe makolo anu adachitira ndi kusokera popembedza milungu yao yonyansa? Pamene mubwera ndi mphatso zanu, ndi kumapereka ana anu kuti akhale nsembe zopsereza, mumadziipitsa potumikira mafano anu ambirimbiri mpaka lero lino. Kodi Aisraele inu, ndingathe kukulolani bwanji kuti mulandire malangizo kwa Ine? Pali Ine ndemwe Chauta wamoyo, sindidzalola zoterezi. Inuyo mukufuna kukhala ngati anthu a mitundu ina, ngati anthu a m'maiko ena amene amapembedza mitengo ndi miyala. Koma zimenezo sizidzachitika konse. “Ine Ambuye Chauta ndikuti, Pali Ine ndemwe wamoyo, ndidzakulamulani ndi dzanja langa lamphamvu, nditasamula mkono wanga ndili wokwiya kwambiri. Ndi dzanja langa lamphamvu ndi mkono wanga wosamula kuwonetsa mkwiyo, ndidzakuchotsani pakati pa mitundu ina ya anthu ndi kukusonkhanitsani kuchokera kumaiko kumene mudabalalikirako. Ndidzakuloŵetsani m'chipululu choyenera akunja. Kumeneko ndidzakuimbani mlandu choonana maso ndi maso. Ndidzakulangani monga momwe ndidalangira makolo anu ku chipululu cha ku Ejipito. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. “Ndidzakuŵerengani ndi ndodo ya mbusa, ndi kukuloŵetsani m'chigwirizano cha chipangano changa. Ndidzakuchotserani anthu amene amandipandukira ndi kundichimwira. Ndidzaŵatulutsa m'dziko limene akukhalamolo, koma sadzapondamo m'dziko la Israele. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta. “Koma inu Aisraele, zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Pitani nonsenu mukatumikire mafano anu! Koma ndithu ndikuti pambuyo pake mudzandimveranso, ndipo simudzaipitsanso dzina langa loyera popereka mphatso kwa mafano anu! Zoonadi Aisraele onse adzanditumikira m'dziko mwaomo ku phiri langa lalitali, phiri loyera la ku Israele. Kumeneko ndidzaŵalandira moŵakomera mtima. Kumeneko ndidzayembekeza kulandira mitulo yao ndi mphatso zao zopambana, pamodzi ndi zopereka zao zopatulika. Inu nomwe ndidzakulandirani ngati nsembe za fungo lokoma, nditakutulutsani pakati pa anthu a mitundu ina, ndi kukusonkhanitsani kuchokera kumaiko kumene mudabalalikira. Pamenepo ndidzaonetsa ungwiro wanga pakati pa inu, ndipo mitundu yonse ya anthu idzaona. Apo mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndikadzakubwezerani kwanu ku dziko la Israele, dziko limene ndidachita kulumbira kuti ndidzapatsa makolo anu. Kumeneko mudzakumbukira makhalidwe anu oipa ndi zonyansa zanu zonse zimene mudadziipitsa nazo. Ndipo mudzamva nyansi ndi inu nomwe chifukwa cha zonse zimene mudachita. Tsono inu a m'banja la Israele mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, pamene ndidzakuchitirani zabwino, osakumbukira makhalidwe anu oipa ndi ntchito zanu zopotoka, kuti choncho dzina langa lilemekezeke. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.” Pambuyo pake Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, tembenuka uyang'ane kumwera, ndipo ulalikire modzudzula anthu akumwera. Uliimbe mlandu dziko lankhalango lakumwera ku Negebu. Uliwuze kuti, Chauta akuti mumvere mau ake, Iye akunena kuti, ‘Ndidzakuyatsa moto, ndipo motowo udzapsereza mitengo yako yonse youma ndi yaiŵisi yomwe. Malaŵi ake adzakhala osazimika, ndipo aliyense kuchokera kumwera mpaka kumpoto adzapsa nawo. Anthu onse adzadziŵa kuti Ine Chauta ndine amene ndauyatsa motowo, ndipo sudzazimidwadi.’ ” Tsono ndidati, “A! Inu Ambuye Chauta, anthu akundinena, akuti, ‘Suja amangonena nthano chabe ameneyu!’ ” Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, tembenuka uyang'ane cha ku Yerusalemu, ndipo ulalike zodzudzula malo ake opatulika. Ulose zodzudzula dziko la Israele. Uliwuze dziko la Israelelo kuti Chauta akuti, ‘Ndimati ndilimbane nawe. Choncho ndidzasolola lupanga langa m'chimake kuti ndiphe anthu ako, abwino ndi oipa omwe. Ndithu ndidzasolola lupanga langa m'chimake kuti ndidzaphe anthu ako oipa ndi abwino omwe, ndiye kuti anthu onse kuyambira kumwera mpaka kumpoto. Motero anthu onse adzadziŵa kuti Ine Chauta ndasolola lupanga langa, ndipo sindidzalilonganso m'chimake.’ “Tsono iwe mwana wa munthu, buula pamaso pao, buula kwambiri ndi mtima woŵaŵa zedi. Akakufunsa chifukwa chake chimene ukubuulira, uŵayankhe kuti, ‘Ndikubuula chifukwa cha nkhani zimene ndamvazi. Zikadzachitika zimenezo, mitima idzangoti fumu, ndipo manja ao onse adzalefuka, mpweya wao wonse udzaŵathera, onse m'maondo mwao mudzangoti zii. Zikubwera, zidzachitikadi!’ Ndikutero Ine Ambuye Chauta.” Chauta adandipatsiranso uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, ulose, ndipo unene kuti Ambuye akuti, “ ‘Lupanga, lupanga, alinola, ndipo alipukuta. Alinola kuti likaphe, alipukuta kuti ling'anipe ngati mphezi. Kodi tingakondwere bwanji, pamene anthu anga anyoza ndodo yanga yolangira? Lupanga laperekedwa kuti alipukute ndipo kuti alinyamule. Lupanga limeneli lanoledwa ndi kupukutidwa, kuti alipereke m'manja mwa munthu amene amapha. Ulire ndipo ufuule, iwe mwana wa munthu, chifukwa zonsezi zidzagwera anthu anga. Zidzagweranso akalonga a Aisraele. Adzaphedwa ndi lupanga pamodzi ndi anthu anga. Nchifukwa chake udzigunde pa chifuŵa mwachisoni. Zingalephere bwanji kuwoneka, popeza kuti akunyoza ngakhale ndodo yanga yolangira?’ Ndikutero Ine Ambuye Chauta. “Koma iwe mwana wa munthu, losa, ndipo uwombe m'manja. Lupangalo lidzagwe kaŵiri ngakhale katatu, ndiye kuti lupanga lophera. Ndilodi lupanga loononga anthu koopsa, limene likuŵazungulira. Anthu anga adzataya mtima, ndipo ambiri adzagwa. Ndaŵaikira lupanga laphuliphuli. Ha, lupanga lidapangidwadi kuti lizing'anipa ngati mphezi, ndipo azilisolola nkuphera anthu. Lupanga iwe, uzikapha ku dzanja lamanja, uzikapha ku dzanja lamanzere, kulikonse kumene nsonga yako yaloza. Inenso ndidzaomba m'manja, ndi kuziziritsa mkwiyo wanga. Ine Chauta ndatero.” Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, ulembe zizindikiro pa miseu iŵiri imene mfumu ya ku Babiloni ingathe kudzeramo, pobwera ndi lupanga. Iŵiri yonseyo idzakhala yochokera ku dziko limodzi. Uike chikwangwani pa mphambano ya miseu yopita ku mzinda. Ulembe zizindikiro pa mseu umene lupanga lidzadzere popita ku Raba wa ku Amoni, ndiponso ku Yuda ndi ku Yerusalemu, mzinda wamalinga. Mfumu ya ku Babiloni yaima ku njira pa mphambano ya miseu. Ikuwombeza maula ndi mivi kuti ipeze njira yoyenera kudzeramo. Ikupempha nzeru kwa milungu yake, ndipo ikuyang'ana chiŵindi cha nyama yopereka ku nsembe. Tsono m'dzanja lake lamanja muli muvi wa ula wolembedwa Yerusalemu. Kumeneko mfumu iyenera kukalalika za kupha anthu ndiponso kufuula mfuu wankhondo. Iyenera kupanga makina othyolera zipata, kuunda mitumbira yankhondo ndi kumanga nsanja. Koma kwa anthu a ku Yerusalemu zidzaoneka ngati zolosa zabodza, chifukwa cha malumbiro amene adaachita kwa mfumuyo. Koma adzaŵakumbutsa za machimo ao, kuti adzatengedwe ukapolo. “Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta, ndikuti, Mwandikumbutsa zolakwa zanu, ndipo kundiwukira kwanu kwaonekera poyera. Mukuwonetsa machimo anu pa zochita zanu zonse. Nchifukwa chake mudzagwidwa ndi kutengedwa ukapolo. “Tsono iwenso, wolamulira Israele, iwe wonyozeka ndi woipa, lafika tsiku lako, ndiye kuti nthaŵi ya chilango chako chomaliza.” Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Vula nduŵirayo, chotsa chisoti chaufumucho. Zonse zasinthika! Otsika uŵakweze, okwera uŵatsitse. Chipasupasu! Chipasupasu! Mzinda ndidzaupasula, ndipo sadzaumanganso mpaka atafika amene ali woyenera kuulandira. Pamenepo ndidzaupatsa kwa iyeyo. “Tsono iwe mwana wa munthu, ulalike kuti, ponena za Aamoni ndi manyozo ao, Ine Chauta ndikuti, “ ‘Lupanga, lupanga alisolola kuti liwononge. Alipukuta kuti liwononge, kuti ling'anipe ngati mphezi. Zimene akuti akuziwona m'masomphenya nzabodza ndiponso maula ao ndi onama. Mudzakhala pamodzi ndi anthu oipa, amene tsiku lao lafika, ndiye kuti nthaŵi ya kulangidwa kwao komaliza. Mulibwezerenso lupanga m'chimake. Ndidzakuweruzani kumalo kumene mudabadwira, ku dziko la makolo anu. Ndidzakukwiyirani ndipo ukali wanga udzakuyakirani. Ndidzakuperekani m'manja mwa anthu ankhanza, amene amadziŵa kuwononga. Mudzakhala ngati nkhuni pa moto. Ena adzakhetsa magazi anu m'dziko mwanu momwe. Palibe amene adzakukumbukiraninso. Ndatero Ine Chauta.’ ” Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukufuna kudzaweruza Yerusalemu? Kudzaweruza mzinda wodzaza ndi anthu opha anzaoŵa? Tsono uudzudzule chifukwa cha machitidwe ake onse onyansa. Unene kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Wadziitanira tsoka iwe mzinda umene umakhetsa magazi a anthu ake ambiri. Ndiwe mzinda umene umadziipitsa ndi mafano amene udadzipangira! Wapalamula chifukwa cha kukhetsa magazi. Wadziipitsa chifukwa cha mafano amene udapanga. Motero wachepetsa masiku ako, ndipo zaka za moyo wako zatha. Nchifukwa chake ndalola kuti mitundu ya anthu ikunyoze, ndipo kuti maiko onse akuseke. Maiko apafupi ndi akutali omwe adzakunyodola, iwe wa mbiri yoipawe ndi wokonda zandeu. “Taona m'mene akuluakulu onse okhala mwa iwe amaphera anthu anzao, aliyense potsata mphamvu zake. Anthu ako akhala akunyoza atate ao ndi amai ao. Akhala akuzunza alendo okhala nawe, akhalanso akusautsa ana amasiye ndi akazi amasiye. Wanyoza zinthu zanga zopatulika, ndipo waipitsa masiku anga a Sabata. Mwa iwe muli ena ochita ugogodi kuti aphe anzao. Mulinso ena odyera zansembe pa zitunda zachipembedzo. Muli anthu enanso ochita zonyansa. Mwa iwe muli ena ogona ndi akazi a atate ao, ndi enanso ovutitsa akazi pa nthaŵi yao yosamba. Ena amachita chigololo ndi akazi a anzao, ena amachita zoipa ndi apongozi ao. Enanso amaipitsa alongo ao, ana a atate ao. Mwa iwe muli ena olandira ziphuphu kuti aphe anzao. Ena amalandira chiwongoladzanja ndi kupezapo phindu pa zimene amakongoza, ena amaopsa anzao kuti apeze phindu. Onsewo andiiŵala Ine. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. “Nchifukwa chake Ine ndichita kuti m'manja bu nkudabwa kwambiri chifukwa cha phindu lako lopeza monyenga, ndiponso chifukwa cha kuphana kumene kumachitika m'kati mwa malinga ako. Kodi mtima wako udzakhala wolimbabe ndiponso manja ako adzakhalabe amphamvu, ndikadzatsiriza kukulanga? Ine Chauta ndatero, ndipo ndidzazichitadi. Ndidzabalalitsa anthu ako pakati pa mitundu ina ya anthu ndi kuŵamwazira ku maiko akutali. Ndimo m'mene ndidzakuchotsere kuipa kwako. Ndidzakunyozetsa pamaso pa mitundu ya anthuyo. Motero udzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.” Tsono Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, Aisraele onse asanduka achabechabe m'maso mwanga. Akulingana ndi mkuŵa, chitini, chitsulo ndi mtovu, zimene zatsala m'ng'anjo atayeretsa siliva. Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikunena kuti, Popeza kuti nonsenu mwasanduka ngati zotsala zachabe, ndidzakusonkhanitsani ku Yerusalemu. Monga muja anthu amasonkhanitsira siliva, mkuŵa, chitsulo, mtovu ndiponso chitini m'ng'anjo, nasonkheza moto kuti uzisungunule, ndimo m'menenso Ine ndidzakusonkhanitsireni ndili wokwiya ndi waukali. Ndidzakuikani m'kati mwa mzinda ndipo ndidzakusungunulirani m'menemo ngati m'ng'anjo. Ndidzakusonkhanitsani mumzindamo ndi kukoleza moto wa mkwiyo wanga, mpaka mutasungunuka. Mudzasungunukadi monga momwe siliva amasungunukira m'ng'anjo. Motero mudzadziŵa kuti Ine Chauta ndakukwiyirani.” Chauta adandipatsiranso uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, uza Yerusalemu kuti iye uja ndi dziko losayeretsedwa, ndiponso losavumbidwa ndi mvula chifukwa cha mkwiyo wanga. Atsogoleri ake ali ngati mikango yobangula pogwira nyama. Apha anthu, alanda chuma ndi zinthu za mtengo wapatali. Akazi ambiri aŵasandutsa amasiye mumzindamu. Ansembe ake omwe aphwanya malamulo anga, ndipo aipitsa zinthu zanga zopatulika. Sasiyanitsa pakati pa zinthu zopatulika ndi zinthu wamba. Sadaphunzitse anthu kusiyana kwake pakati pa zoyenera pa chipembedzo ndi zosayenera. Sasamala masiku anga a Sabata, motero anthu sandilemekeza. Atsogoleri ake ali ngati mimbulu yokadzula nyama. Amakhetsa magazi ndi kuwononga moyo wa anthu, kuti apate phindu loipa. Ndipo aneneri ake abisa zimenezi monga muja amachitira anthu popaka njereza, amaziphimba ndi zimene amaona m'maloto ao abodza ndi m'maula ao onama. Amati, ‘Ambuye Chauta akunena zakutizakuti,’ pamene Ine Chauta sindidalankhule konse. Anthu am'dzikomo amasautsa anzao ndiponso amaba. Amazunza osoŵa ndi osauka. Amavutitsa alendo posaŵachitira zinthu mwachilungamo. Ndidafunafuna munthu pakati pao woti amange linga, woti pamaso panga aime pamene padagumuka, kuti ateteze dziko ndi kundipepesa kuti ndisaliwononge. Koma munthu woteroyo sindidampeze. Nchifukwa chake ndidaŵakwiyira kwambiri. Ndidzaŵaononga kotheratu ndi mkwiyo wanga woyaka ngati moto. Motero ndidzaŵalanga monga kuŵayenera.” Ndikutero Ine Ambuye Chauta. Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, panali akazi aŵiri, ana a mimba imodzi. Ankachita zadama ku Ejipito. Zadamazo ankachita akali atsikana. Kumeneko anthu ankangoŵasisita pa chifuwa ndi kumaŵagwira maŵere ao osagwa aja. Wamkulu anali Ohola, mng'ono wake anali Oholiba. Ndidaŵakwatira ndipo adandibalira ana aamuna ndi ana aakazi. ‘Ohola’ ndiye Samariya. ‘Oholiba’ ndiye Yerusalemu. “Ohola ankachita zadama ngakhale pamene anali wanga. Ankakangamira zibwenzi zake za ku Asiriya. Amuna amenewo ena anali asilikali ovala zamlangali, ena anali abwanamkubwa, ena atsogoleri a nkhondo, onsewo anyamata osiririka, kudzanso okwera pa akavalo. Oholayo ankachita zadama ndi onsewo, amuna otchuka a ku Asiriya. Ndipo anakadziipitsa ndi mafano a amuna onse amene ankachita naye zadama. Sadasiye makhalidwe ake a dama amene adaŵaphunzira ku Ejipito, kumene amuna ankagona naye akadali namwali. Ankamugwira maŵere akali anthete, namachita naye chigololo. Nchifukwa chake ndidampereka kwa zibwenzi zakezo, ndiye kuti Aasiriya, amene iye adaaŵakangamira. Iwowo adamuvula. Adamulanda ana ake aamuna ndi aakazi, ndipo adamupha ndi lupanga. Atalangidwa choncho, adasanduka chinthu chonyozeka pakati pa akazi onse. “Tsono Oholiba mng'ono wake uja adatengerako, ndipo adachita zadama kupambana mkulu wake. Iyenso ankakangamira Aasiriya, makamaka abwanamkubwa, atsogoleri a nkhondo, asilikali ovala zamlangali, okwera pa akavalo, onsewo anyamata osiririka. Ndidaona kuti iyenso adadziipitsa, ndipo aŵiriwo adatsata njira imodzi. “Koma Oholiba uja adachita chigololo kopitirira mkulu wake. Adaona zithunzi za amuna pa makoma, zithunzi za Ababiloni zolembedwa ndi utoto wofiira. Anthuwo adaamanga malamba m'chiwuno, ndi kuvala nduŵira kumutu. Onse ankaoneka ngati atsogoleri ankhondo, ndipo ankaoneka ngati Ababiloni, mbadwa za ku Kaldeya. Atangoŵaona, mkazi uja adayamba kuŵalakalaka. Motero adatuma amithenga ku Babiloni kukaŵaitana. Choncho amuna a ku Babiloni adabwera kwa iye nagona naye. Mwa chilakolako chao adamuipitsa kaŵirikaŵiri. Koma iwowo atamuipitsa choncho, iye adanyansidwa nawo. Mkaziyo ankachita zadama poyera, ndipo ankaonetsa maliseche ake osachita manyazi. Motero ndidanyansidwa naye monga momwe ndidachitira ndi mkulu wake. Koma ankachitabe zadama zake osalekeza, namakumbukira zadama zimene ankachita pamene anali hule ku Ejipito pa ubwana wake. Ankalakalaka abwenzi ake amene ziwalo zao zinali zazikulu ngati za bulu, amene kutentha kwao kunali ngati kwa akavalo. Motero iwe Oholiba udafuna kuchitanso zadama monga unkachitira ku Ejipito ukadali namwali, kumene ankakusisita pa chifuwa, nkumakugwira maŵere ako osagwa aja. “Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Iwe Oholiba, ndidzakuutsira zibwenzi zako zimene udanyansidwa nazozo kuti zilimbane nawe. Ndidzaziitana kuti zibwere kwa iwe kuchokera ku mbali zonse Ndidzaitana anthu a ku Babiloni, onse a ku Kaldeya, onse amene ali ku Pekodi, a ku Sowa, a ku Kowa, pamodzi ndi Aasiriya onse. Onsewo ndi amuna osiririka, abwanamkubwa, atsogoleri a nkhondo, asilikali, onsewo ndi okwera pa akavalo. Adzabwera kuchokera kumpoto kudzakuthira nkhondo ndi akavalo ankhondo, magaleta ndi ngolo zambiri, ndiponso gulu lalikulu la ankhondo ochokera ku maiko onse. Adzakuzinga mbali zonse atavala malihawo, zishango ndi zisoti zankhondo. Ndidzakupereka m'manja mwao kuti akulange. Ndipo adzakulangadi monga momwe adzafunire iwowo. Ndidzaŵalola kuti akuchite zankhanza chifukwa choti ndakukwiyira. Adzakudula mphuno ndi makutu, ndipo otsalira mwa iwe adzaŵapha ndi lupanga. Adzakulanda ana ako aamuna ndi aakazi, ndipo amene adzatsalira mwa iwe adzapsa ndi moto. Adzakuvula zovala, ndipo adzakukolopola zodzikongoletsera zako za mtengo wapatali. Motero ndidzaletsa zonyansa zako ndi zigololo zako zimene wakhala ukuchita kuyambira nthaŵi imene unali ku Ejipito. Choncho sudzalakalakanso za ku Ejipito kapena kuzikumbukira. “Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ndikukupereka m'manja mwa adani ako, amene udaŵafulatira chifukwa choipidwa nawo. Ndipo adzakuchita zachidani. Adzakulanda zonse zimene udapeza ndi dama lako, ndipo adzakusiya wamaliseche ndi wausiŵa. Thupi limene unkachitira zadama lidzakhala lamaliseche. Zonyansa zako ndi chigololo chako, ndizo zakubweretsera zimenezi, chifukwa choti wachita zonyansa ndi mitundu ya anthu achilendo, ndi kudziipitsa ndi mafano ao. Udatsanzira zochita za mkulu wako, ndipo ndidzaika chikho cha chilango chake m'manja mwako.” “Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Udzamwera chikho cha mkulu wako, chikho choloŵa ndiponso chachikulu. Anthu adzakuseka ndi kukunyoza, chifukwa chikhocho nchodzaza kwambiri. Udzaledzera, ndipo mumtima mwako mudzadzaza ndi chisoni. Chimenechi ndi chikho choopsa ndi chachipasupasu, chikho chachilango cha mbale wako Samariya. Udzachimwa chikhocho mpaka kuchigugudiza. Tsono udzachitafuna, ndipo udzang'amba maŵere ako ndi zigoba zake. Ineyo ndanena zimenezi. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.” “Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Chifukwa chakuti wandiiŵala Ine ndi kundifulatira, uyenera kulangidwa chifukwa cha zonyansa zako ndi zigololo zako.” Chauta adandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukufuna kudzaweruza Ohola ndi Oholiba? Tsono uŵaimbe mlandu chifukwa cha zonyansa zao zimene adachita. Adachita chigololo, ndipo adapha anthu. Adachita chigololo popembedza mafano ao, ndipo ana anga amene adandibalira, adaŵapereka kwa mafanowo ngati chakudya chao. Adachitanso izi: adaipitsa malo anga ondipembedzera, ndipo adanyoza masiku anga a Sabata. Adangoti atapereka ana ao nsembe kwa mafano ao, nthaŵi yomweyo nkuloŵa m'Nyumba yanga yoyera naiipitsa. Ndithu zimenezi nzimene adachita m'Nyumba mwanga. “Komanso adatuma amithenga kukaitana amuna akutali. Anthuwo atabwera, abale aŵiri aja adasambasamba, nkukometsa m'masomu ndi utoto, navala zamakaka. Adakhala pa bedi lokongola, ndipo patsogolo pao panali tebulo. Patebulopo adaikapo lubani ndi mafuta, zonse zoŵapatsa Ine. Mfuu wa chigulu cha anthu udamveka. Kuwonjezera pa anthu wamba, panalinso ena oledzera ochokera ku chipululu. Adaveka akaziwo makoza kumanja ndiponso zisoti zaufumu zokongola ku mutu. “Tsono Ine ndidati, ‘Mkazi ameneyu ndi wotheratu ndi chigololo. Koma onani, anthu akutsatabe zadama zake zomwezo. Choncho adapita kwa iye monga m'mene anthu amapitira kwa mkazi wadama. Ndimo adapitira kwa Ohola ndi kwa Oholiba kukachita nawo zadama. Koma tsiku lina anthu abwino adzaŵazenga anthuwo mlandu wa chigololo ndi wa kupha anzao. Zoonadi ngachigololo, ndipo m'manja mwao magazi ali psu.’ “Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Itanani chigulu cha anthu, kuti chiŵazunze ndi kulanda chuma chao. Akazi aŵiriwo aŵaponye miyala ndi kuŵatema ndi malupanga ao. Aphenso ana ao aamuna ndi aakazi ndipo atenthe nyumba zao. Motero ndidzathetsa chiwerewere m'dziko lao, ndipo akazi onse adzaphunzira kuti asadzachite zonyansa ngati iwowo. Adzalangidwa chifukwa cha makhalidwe ao achiwerewere, ndipo adzazunzika chifukwa cha tchimo la kupembedza mafano. Tsono adzadziŵa kuti Ine ndine Ambuye Chauta.” Pa tsiku lakhumi la mwezi wakhumi, chaka chachisanu ndi chinai cha ukapolo, Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, lemba dzina la tsiku lalero, lero lomwe lino. Lero ndilo tsiku limene mfumu ya ku Babiloni yazinga Yerusalemu ndi zithando zankhondo. Uŵaphere mwambi anthu aupanduŵa. Uŵauze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, “ ‘Ikani mphika pa moto, ndipo muthiremo madzi. Mumphikamo muikemo nthuli za nyama, nthuli zabwino kwambiri za mwendo wathako ndi mwendo wamwamba. Mudzazemo mafupa abwino. Pa gulu la nkhosa musankhulepo nkhosa yabwino kwambiri, ndipo muike nkhuni pansi pa mphikawo. Madziwo aŵire, kenaka muphike nyama ija pamodzi ndi mafupa omwe’. “Tsono zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Tsoka kwa mzinda wamagaziwe, tsoka kwa mphika wa dzimbiri lokangamira ndi losachoka. Mutulutsemo nthuli imodziimodzi, osasankhula. Magazi amene adakhetsa mumzindamo akadali pakati pake, chifukwa adaŵataya pa thanthwe losalala osati pa dothi, kuti fumbi lingaŵafotsere. Ndidaŵasiyadi magaziwo pa mwala wambee, kuti asafotsereke, chifukwa chofuna kuwonetsa mkwiyo wanga ndi kulipsira. “Tsono Ine Ambuye Chauta ndikuti, Tsoka kwa mzinda wamagaziwo! Inenso ndidzayatsa chimulu chachikulu cha nkhuni. Onjeza nkhuni, usonkhe moto, uphike nyama, uiphike bwino, utsanyule msuzi, ndipo upsereze mafupa. Tsono uike pa makala mphika wopanda kanthuwo, kuti chitsulo chake chipse, kuchita kuti psuu. Zonyansa zake zonse zisungunuke, dzimbiri lichoke. Koma nkuuyeretsa bwanji? Dzimbiri lake lidaloŵerera, silingathe kuchoka ngakhale ndi moto womwe. Dzimbiri limeneli ndi zilakolako za dama lako, poti nditakutsuka sudayere. Tsono sudzayeranso mpaka mkwiyo wanga utakwaniratu pa iwe. Ine Chauta ndalankhula zimenezi. Zilikudza ndipo ndidzazichitadi. Sindidzabwerera m'mbuyo, sindidzakulekerera kapena kukhululuka ai. Ndidzakulanga potsata makhalidwe ako ndi zimene udachita. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.” Chauta adandipatsiranso uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, ndikulanda mwadzidzidzi mkazi wako amene amakukomera m'maso kwambiri. Koma usadandaule, usalire kapena kukhetsa misozi. Udzume, koma m'chikatikati, usabume maliro. Nduŵira yako uvale ndithu, nsapatonso uvale. Usaphimbe kumaso kapena kudya chakudya cha olira.” Choncho ndidalankhula ndi anthu m'maŵa, madzulo mkazi wanga nkumamwalira. M'maŵa mwake, ndidachita monga momwe adandilamulira. Anthu adandifunsa kuti, “Bwanji osatifotokozera tanthauzo lake la zimene ukuchitazi? Kodi ukuchitiranji zotere?” Ndidaŵayankha kuti, “Chauta adandipatsira uthenga uwu, adati, ‘Uza Aisraele mau anga akuti, Ndidzaipitsa Nyumba yanga imene mwakhala mukuinyadira kwambiri. Mumakondwa kwambiri poiwona, ndipo mumaikonda ndi mtima wonse. Ana anu aamuna ndi aakazi amene mudaŵasiya m'mbuyo, adzaphedwa ndi lupanga.’ Koma inu mudzachita monga ndachitira inemu. Simudzaphimba kumaso, kapena kudya chakudya cha anthu olira. Nduŵira mudzavala ndithu ku mutu, nsapatonso mudzavala. Simudzalira maliro kapena kukhetsa misozi. Koma mudzavutika zedi chifukwa cha machimo anu, ndipo muzidzangodzumirana. Tsono ine Ezekielene ndidzakhala chitsanzo kwa inu, mudzachita monga momwe ine ndachitira. Chauta akuti zimenezi zikadzachitika, mudzadziŵa kuti Iye ndi Ambuye Chauta.” Pambuyo pake Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, tsiku lina anthuŵa ndidzaŵachotsera linga lao limene ankakondwerera kukongola kwake, limene linkaŵakomera m'maso poliwona, limenenso ankaikapo mtima kwambiri. Ndidzaŵachotseranso ana ao aamuna ndi aakazi. Pa tsiku limenelo wopulumuka adzabwera kudzakuuza zimenezo. Pa tsiku lomwelo udzathanso kulankhula, choncho udzalankhula naye wopulumukayo, sudzakhalanso bububu. Motero udzakhala chizindikiro kwa iwo, ndipo adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.” Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, tembenukira kwa anthu a ku Amoni, ulalike zoŵadzudzula. Unene kuti, inu Aamoni, imvani mau a Ambuye Chauta akuti, ‘Paja mudatchula mau onyodola, mutaona malo anga opatulika akuipitsidwa, nthaka ya Israele itaguga, ndipo anthu a ku Yuda atatengedwa ukapolo. Nchifukwa chake ndidzakuperekani m'manja mwa anthu akuvuma. Adzakhoma mahema ao ndi kumanga nyumba zao m'dziko mwanu. Adzakudyerani zipatso zanu, adzakumwerani mkaka wanu. Ndidzasandutsa Raba kuti akhale busa la ngamira, ndipo ndidzasandutsa mizinda ya Aamoni kuti ikhale makola a nkhosa. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta. Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Mudaomba m'manja ndi kulumphalumpha mokondwa, ndipo mudanyodola dziko la Israele ndi kulinyoza ndi mtima wonse. Nchifukwa chake Ine ndidzakukanthani ndi dzanja langa ndipo ndidzakuperekani kuti mukhale chofunkha cha mitundu ina ya anthu. Ndidzakuchotsani pakati pa mitundu ina ya anthu, ndipo ndidzakufafanizani pa dziko lapansi. Ndidzakuwonongeranitu, ndipo mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.’ “Mau a Ine Ambuye Chauta ndi aŵa: Chifukwa choti Mowabu adanena kuti a ku Yuda ali ngati anthu ena onse, ndidzagumula mbali ina ya Mowabu, ndidzaononga mizinda yake yakumalire, ndiye kuti mizinda ija yokongola kwambiriyi ya Beteyesimoti, Baala-Meyoni ndi Kiriyataimu. Ndidzapereka Amowabu pamodzi ndi Aamoni m'manja mwa mitundu yakuvuma, kotero kuti Aamoni adzaiŵalikiratu pakati pa mitundu ya anthu. Amowabunso ndidzaŵalangadi. Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.” “Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Chifukwa choti Edomu adalipsira Yuda mwankhanza, adapalamula kwambiri pakutero. Choncho Edomuyo ndidzamkantha ndi dzanja langa, ndipo ndidzaononga anthu pamodzi ndi nyama zomwe kumeneko. Dzikolo ndidzalisandutsa chipululu kuyambira ku Temani mpaka ku Dedani. Anthu ambiri adzaphedwa pa nkhondo. Ndidzalanga Edomu ndi dzanja la anthu anga Aisraele. Adzamchita monga m'mene mkwiyo wanga ndi ukali wanga udzafunire. Choncho adzaona kulipsira kwanga. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. “Mau a Ine Ambuye Chauta ndi aŵa: Afilisti adalanga anthu anga mwankhanza ndi kuŵalipsira ndi mtima wonyoza ndi wofuna kuŵaononga malinga ndi chidani chao chachikhalire. Nchifukwa chake Afilistiwo ndidzaŵakantha ndi dzanja langa. Ndidzafafaniza Akereti ndi kuwononga ena onse okhala m'mbali mwa nyanja. Ndidzaŵalipsira koopsa ndi kuŵalanga mwaukali kwambiri. Ndikadzaŵalanga choncho, adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.” Pa chaka cha khumi ndi chimodzi cha ukapolo, tsiku loyamba la mwezi, Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, anthu a ku Tiro adanyodola Yerusalemu kuti, ‘Ha! Uja adaali chipata choloŵerapo mitundu ya anthuyu, waonongeka. Zipata zake zatitsekukira ife tsopano. Tilemera, poti iye tsopano wasanduka bwinja.’ “Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndikukukana iwe Tiro. Ndipo ndidzakubweretsera anthu a mitundu yambiri kuti adzalimbane nawe, monga momwe mafunde am'nyanja amaŵindukira. Anthuwo adzaononga malinga a Tiro ndi kugwetsa nsanja zake. Ndidzapala dothi lake, ndi kumsandutsa thanthwe lambee. Adzakhala malo oyanikapo kombe pakati pa nyanja. Mau anga ndi amenewo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. Adzasanduka chofunkha cha anthu a mitundu ina. Anthu a m'midzi yake yakumtunda adzaphedwa pa nkhondo. Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta. “Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Iwe Tiro ndidzakubweretsera Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mfumu ya mafumu, kuchokera kumpoto. Adzabwera ndi akavalo ndi magaleta, ndiponso okwera pa akavalo ndi gulu lalikulu lankhondo. Anthu a m'midzi yako yakumtunda adzaŵapha pa nkhondo. Adzakuzinga ndi zithando zankhondo, ndiponso ndi ziwundo zankhondo. Adzakukwezera zishango kuti alimbane nawe. Adzagwetsa malinga ako ndi makina ogumulira, ndipo adzagwetsa nsanja zako ndi nkhwangwa zake. Akavalo ake ochuluka adzakukwirira ndi fumbi lao. Malinga ako adzagwedezeka ndi mdidi wa akavalo ndiponso ndi mkokomo wa mikombero ya magaleta poloŵa pa zipata zako, monga momwe zimachitikira poloŵa mu mzinda umene wagumulidwa. Akavalo ake adzapondereza miseu yako yonse ndi ziboda zao. Anthu ako adzaŵapha ndi lupanga. Mizati yako yolimba adzaigwetsa. Adzafunkha chuma chako ndi kulanda malonda ako. Malinga ako adzaŵagumula, ndipo nyumba zako zokongola adzazigwetsa. Miyala yako, mitengo yako ndi dothi lako lomwe adzaziponya m'nyanja. Motero ndidzaletsa phokoso la nyimbo zako, ndipo kulira kwa apangwe ako sikudzamvekanso. Ndidzakusandutsa thanthwe lambee. Udzasanduka malo okayanikapo kombe, ndipo sudzamangidwanso. Ine Chauta ndalankhula. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. “Zimene Ine Ambuye Chauta ndikukuuza iwe mzinda wa Tiro ndi izi: Nyanja idzagwedezeka pamodzi ndi zilumba, pakumva za kugwa kwako, ndiponso poona opweteka akubuula, ndipo anthu akuphedwa pakati pako. Pamenepo mafumu onse akunyanja adzatsika pa mipando yao yaufumu. Mikanjo yao adzaiika pambali, ndipo adzavula zovala zao zopetapeta zija. Adzachita mantha nakhala pansi akunjenjemera kosalekeza, ndipo adzangoti pakamwa gwirire poona zimene zakugwera. Apo adzayamba kuimba nyimbo yokudandaulira. Adzati, “ ‘Mzinda wotchuka iwe, nkuchita kuwonongeka chotere! Unali wamphamvu pa nyanja, iweyo ndi anthu ako. Iweyo ndi anthu ako munkaopsa anthu a m'mbali mwa nyanja. Tsopano maiko a m'mbali mwa nyanja akunjenjemera chifukwa cha kugwa kwako. Nawonso okhala ku zilumba agwidwa ndi mantha chifukwa cha kutha kwako.’ “Mau a Ine Ambuye Chauta ndi aŵa: Ndidzakusandutsa bwinja, ngati mzinda umene munthu sangathe kukhalamo. Ndidzakuphimba ndi madzi ozama am'nyanja, madzi amphamvu oti akumize. Ndidzakugwetsa pansi kuti ukhale pamodzi ndi anthu amvulazakale amene akutsikira ku manda. Ndidzakusunga kudzenjeko ngati ku bwinja losiyidwa kalekale, pamodzi ndi anthu amene adafa kale. Motero sudzakhalanso ndi anthu m'dziko la amoyo. Ndidzakuthetsa mochititsa mantha, ndipo sudzakhalaponso. Ngakhale anthu adzakufunefune, sadzakupezanso. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.” Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, uimbe nyimbo yodandaulira Tiro. Uuze Tiro, mzinda wokhala pa dooko la nyanja, umene umachita malonda ndi anthu a mitundu yambiri ya ku maiko ambiri a m'mbali mwa nyanja, kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: “ ‘Iwe Tiro, wakhala ukunena kuti, “Ndine wokongola kwabasi.” Malire ako ali m'kati mwenimweni mwa nyanja. Amisiri amene adakumanga, adakumanga ngati chombo chochititsa kaso zedi. Adakupanga ndi matabwa a mitengo ya paini ya ku phiri la Seniri. Adatenga mkungudza ku Lebanoni kuti adzapangire mlongoti wako. Adapanga nkhafi zako ndi mtengo wa thundu wa ku Basani. Adapanga thandala lako ndi matabwa a mitengo ya paini ya ku zilumba za Kitimu, pakati pa matabwawo panali zosema za minyanga ya njovu. Thanga lako linali la nsalu yabafuta. Nsalu yake inali yopeta bwino, yochokera ku Ejipito, ndipo ndiyo inali ngati mbendera yako. Nsalu zophimba mahema ako zinali zobiriŵira ndi zofiirira, zochokera ku zilumba za Elisa. Anthu a ku Sidoni ndi a ku Arivadi ndiwo amene ankakupalasa. Akatswiri ako, iwe Tiro, anali mwa iwe, ndiwo amene ankakuyendetsa. Mwa iwe munalinso akuluakulu ndi akatswiri a ku Gebala, amene ankakonza ziboo zako. Amalinyero ambiri m'zombo zao ankadzakuyendera kuchokera ku maiko onse kudzachita nawe malonda.’ “Anthu a ku Persiya, a ku Ludi ndi a ku Puti adaloŵa m'gulu la ankhondo ako. Ankapachika zishango zao ndi zisoti m'kati mwako, ndipo potero ankakupatsa ulemerero. Ankhondo a ku Arivadi ndi a ku Heleki ankalonda malinga ako ponse pozungulira. Anthu a ku Gamadi ankakwera pa nsanja zako, ndi kukapachika zishango zao pa malinga ako ponse pozungulira. Amenewo ndiwo amene ankakukongoletsa kwabasi. “Dziko la Tarisisi linkachita nawe malonda chifukwa cha katundu wako wamtundumtundu, ndipo unkagulako siliva, chitsulo, chitini ndi mtovu, mosinthana ndi katundu wako. Yavani, Tuba ndi Meseki ankachita nawe malonda. Ankakugulitsa akapolo ndi ziŵiya zamkuŵa mosinthana ndi katundu wako. Anthu a ku Betetogarima ankapereka akavalo antchito, akavalo ankhondo ndi abulu mosinthana ndi katundu wako. Anthu a ku Dedani ankachita nawe malonda, anthunso a m'mbali mwa nyanja ankakupatsa minyanga ya njovu ndi phingo mosinthana ndi katundu wako. Anthu a ku Aramu ankagula zinthu zambiri zamalonda mosinthana ndi katundu wako wochuluka. Iwo ankapereka miyala ya emeradi, nsalu zofiirira, nsalu zopetapeta, nsalu zabafuta, korale ndi miyala ya rubi, mosinthana ndi katundu wako. Yuda ndi Israele ankagula malonda ako. Iwo ankapereka tirigu, zipatso za olivi, nkhuyu zoyamba, ndiponso uchi, mafuta aolivi ndi zonunkhira zokometsera chakudya, mosinthana ndi katundu wako. Anthu a ku Damasiko ankagula kwa iwe chifukwa cha kuchuluka kwa zamalonda zako ndi katundu wako wosiyanasiyana. Ankakugulitsa vinyo wa ku Heliboni ndi ubweya wa nkhosa wambee. Ankaperekanso vinyo wa ku Uzala, ndiponso zitsulo zosalala, kasiya ndi bango lonunkhira, kusinthitsa ndi malonda ako. Anthu a ku Dedani ankakugulitsa nsalu zoika pa zishalo za akavalo. Arabiya ndi mafumu onse a ku Kedara ankachita nawe malonda mosinthana ndi ana a nkhosa, nkhosa zamphongo ndi mbuzi. Amalonda a ku Sheba ndi a ku Rama ankagulanso kwa iwe. Ankapereka zonunkhira zabwino kwambiri, miyala ya mtengo wapatali ndi golide yemwe, mosinthana ndi katundu wako. Mizinda iyi ya Harani, Kane, Edeni, Asuri ndi Kilimade inkachita nawe malonda. Anthu akumeneko ankasinthitsana nawe zovala zabwino kwambiri, nsalu zofiirira, nsalu zopetapeta, makalipeti amaŵangamaŵanga, zonsezo atazimanga bwino ndi zingwe zolimba. Zombo za ku Tarisisi zinkanyamula malonda ako. “Motero iweyo unali ngati chombo chapanyanja chodzaza ndi katundu wolemera. Opalasa ako adakupititsa ku nyanja yozama, kumene mphepo yakuvuma idakukankhira nikumiza m'kati mwa nyanja. Chuma chako, katundu wako ndi malonda ako, amalinyero ako ndi oongolera omwe, amisiri a matabwa a zombo zako ndiponso oyendetsa malonda ako, asilikali ako onse amene anali m'katimo, ndi gulu lonse lankhondo pakati pako, onsewo adamira m'nyanja tsiku limene udaonongeka. Chifukwa cha kufuula kwa amalinyerowo, kumtunda kudagwedezeka. Onse amene amapalasa chombo, atuluka m'zombo zao. Amalinyero onse ndi oongolera omwe aimirira ku mtunda. Onsewo akukulira iweyo, kulira kwake kwambiri. Akudzithira fumbi kumutu, nkumamvimvinizika pa phulusa. Akudzimeta mpala chifukwa cha iwe, ndipo akuvala ziguduli. Akulira ndi mitima yoŵaŵa. Akukuimbira nyimbo yodandaula, akuti, ‘Ndani adaonongedwapo ngati Tiro, pakati pa nyanja?’ Pamene malonda ako ankaoloka nyanja, unkakondweretsa mitundu yambiri ya anthu pa zosoŵa zao. Mafumu a dziko lapansi adalemera nacho chuma chako. Koma tsopano wathyokera m'nyanja, pansi penipeni pa nyanja. Kungoti iweyo, katundu wako ndi antchito ako onse, nonse mwathera pamodzi m'nyanja. Aliyense amene amakhala m'mbali mwa nyanja waopsedwa nazo zimene zakuchitikira. Mafumu ao akuchita mantha, nkhope zao zasinthika ndi mantha. Anthu amalonda a ku maiko ena akukunyodola tsopano. Watha mochititsa mantha, sudzakhalaponso mpaka muyaya.” Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, uza mfumu ya ku Tiro mau angaŵa akuti, Iwe ndi mtima wako wodzikuza umanena kuti, ‘Ine ndine mulungu. Ndimakhala ngati mfumu pa mpando wa milungu pakati pa nyanja yozama.’ Koma chonsecho ndiwe munthu chabe, osati mulungu, ngakhale umadziyesa wanzeru ngati mulungu. Ai, iwe ndiwe wanzerudi kupambana Daniele, palibe chinsinsi chobisika kwa iwe. Nzeru zako ndi kumvetsa kwako zidakulemeretsa pokupatsa chuma cha golide ndi siliva. Udachulukitsa chuma chako chifukwa cha nzeru zako zoyendetsera malonda, ndipo ukunyada chifukwa cha chuma chakocho. Tsono Ine Ambuye Chauta ndikuti, Poti umadziganizira kuti ndiwe wanzeru ngati mulungu, Ine ndidzabwera ndi anthu achilendo kuti adzalimbane nawe. Iwowo ndi mtundu wa anthu ankhanza kwambiri. Adzakuthira nkhondo kuti aononge zokoma zonse zimene udazipata ndi nzeru zako, ndiponso kuti athyole kunyada kwako. Adzakuponya ku malo a anthu akufa, udzafa imfa yoopsa m'nyanja yozama. Kodi pamenepo udzanenabe kuti ndiwe mulungu pamaso pa anthu amene akukuphawo? Iyai, udzaoneka ngati munthu ndithu osati mulungu, pamene udzakhala m'manja mwa okuphawo. Udzafa imfa ya anthu osaumbalidwa m'manja mwa anthu achilendo. Ine ndalankhula zimenezi. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.” Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo ya maliro, kulira mfumu ya ku Tiro. Uiwuze mau angaŵa akuti, Udaali chitsanzo cha ungwiro weniweni. Udaali wanzeru ndiponso wokongola kwabasi. Unkakhala ngati ku Edeni, ku munda wa Mulungu, ndipo unkadzikongoletsa ndi miyala yamtengowapatali ya mitundu yonse: karineliyoni, topazi, jasipere, kirisoliti, berili, onikisi, safiro, rubi ndi emeradi. Zoikamo miyalayo zinali zagolide. Adakupangira zonsezi pa tsiku limene udalengedwa. Ndidakuikira mngelo woopsa kuti azikulonda. Unkakhala pa phiri langa lopatulika, ndipo unkayenda pakati pa miyala yamoto. Makhalidwe ako anali angwiro kuyambira tsiku limene udalengedwa mpaka nthaŵi imene udayamba kuchita zoipa. Potanganidwa ndi zamalonda, udaachulukitsa zandeu ndi kumangochimwa. Nchifukwa chake ndidakuchotsa ku phiri langa lopatulika. Mngelo amene ankakulonda adakupirikitsa kuchokera ku miyala yamotoyo. Unkanyada chifukwa cha kukongola kwako, udaipitsa nzeru zako chifukwa chofuna kukhala wotchuka. Motero ndidakugwetsa pansi kuti ukhale chenjezo kwa mafumu ena. Udachita zoipa zambiri pa kugula ndi kugulitsa zinthu, ndipo choncho malo ako achipembedzo udaŵaipitsa. Motero ndidabutsa moto pakati pako ndi kukupserezeratu. Onse okupenya tsopano amaona kuti ndiwe phulusa pa dziko lapansi. Anthu a mitundu yonse amene ankakudziŵa akuwopsedwa ndi zimene zidakuchitikira. Imfa yako inalidi yoopsa, ndipo sudzakhalanso mpaka muyaya.” Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, utembenukire ku mzinda wa Sidoni ndipo ulose momdzudzula kuti, “Ine Ambuye Chauta ndikuti, ‘Ndine mdani wako, iwe Sidoni, ndipo anthu akadzaona zimene ndidzakuchite iwe, adzandilemekeza. Adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndikadzakulanga ndipo ndikadzaonetsa pakati pako kuti Ine ndine woyera. Ndidzakugwetsera mliri, ndipo m'miseu yako mudzayenderera mitsinje ya magazi. Anthu adzatha phu nkuphedwa, nkhondo idzakuzinga mbali zonse. Tsono anthu adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.’ ” “Nthaŵi imeneyo pafupi ndi Aisraele sipadzakhalanso anthu onyoza omaŵalasa ngati mitungwi, kapena omaŵapweteka ngati minga. Apo anthu adzadziŵa kuti Ine ndine Ambuye Chauta. “Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Nditasonkhanitsa Aisraele kuchokera ku mitundu ya anthu kumene adamwazikira, ndidzaonetsa kuyera kwanga mwa iwo, anthu a mitundu yonse akuwona. Aisraelewo adzakhalanso m'dziko lao limene ndidaapatsa mtumiki wanga Yakobe. Adzakhala kumeneko mwamtendere, ndipo adzamanga nyumba ndi kulima minda yamphesa. Adzakhala kumeneko mwamtendere, pamene ndidzalange anthu oyandikana nawo, amene ankaŵanyoza. Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, Mulungu wao.” Pa tsiku lakhumi ndi chiŵiri la mwezi wakhumi, chaka chakhumi cha ukapolo, Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, umuimbe mlandu Farao, mfumu ya ku Ejipito, ndipo ulose modzudzula iyeyo pamodzi ndi dziko lake lonse. Umuuze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, “ ‘Ndikukuimba mlandu iwe Farao mfumu ya ku Ejipito, iwe ching'ona chogona m'mitsinje mwako. Wanena kuti, mtsinje wa Nailo ndi wako, udaulenga ndiwe. Koma ndidzakukola ndi mbedza m'kamwa mwako, nsomba za m'mitsinje mwako zidzakangamira ku mamba ako. Tsono ndidzakutulutsa mumtsinjemo pamodzi ndi nsomba zimene zakukangamira. Ndidzakutaya ku chipululu, iweyo pamodzi ndi nsomba za m'mitsinje yako. Udzagwera ku thengo popanda wina wokutola kuti aike maliro ako. Ndidzakusandutsa chakudya cha zilombo ndi mbalame.’ “Motero onse okhala ku Ejipito adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta. Iwe Ejipito unali ngati ndodo yabango kwa Aisraele. Ndodoyo idaphwanyikira m'manja ataigwira, ndipo idaŵacheka pa mapewa. Ataitsamira, iyo idathyoka, ndipo m'chiwuno mwao monse mudagwedezeka. “Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndikubweretsera nkhondo kuti idzaononge anthu pamodzi ndi nyama zomwe. Dziko la Ejipito lidzasanduka chipululu, lopanda anthu. Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta. “Zoona, iwe udati, ‘Nailo ndi wanga, ndidamlenga ndine.’ Tsono Ine ndikudana ndi iweyo, pamodzi ndi mitsinje yakoyo. Ndipo Ejipito ndidzamsandutsa bwinja, kuyambira ku mzinda wa Migidoli mpaka ku mzinda wa Siyene, kukafika ku malire a Etiopiya. Palibe phazi la munthu kapena la nyama limene lidzapondapo. Kudzakhala kopanda anthu pa zaka makumi anai. Dziko la Ejipito ndidzalisandutsa bwinja kupambana mabwinja a maiko ena onse. Pa zaka makumi anai mizinda yakenso idzakhala yopasuka kupambana mizinda ina yopasuka. Aejipitowo ndidzaŵamwaza pakati pa mitundu ya anthu, ndi kuŵabalalitsa pakati pa maiko ena. “Komabe Ine Ambuye Chauta ndikuti, Pomatha zaka makumi anaizo, ndidzasonkhanitsa Aejipito kuchokera ku mitundu ya anthu kumene adamwazikira. Ndidzaŵachotsa ku ukapolo, ndipo ndidzaŵabwezera ku Patirosi kumene adachokera. Kumeneko adzakhala ndi ufumu wotsika. Ufumuwo udzasanduka wofooka kupambana maufumu ena onse, ndipo sudzadzikuzanso pakati pa mitundu ya anthu. Ndithudi Aejipito ndidzaŵachepetsa kwambiri, kotero kuti sadzatha kulamuliranso mitundu ina. Aisraele sadzadaliranso Ejipito. Ndipo chilango chimenechi chidzaŵakumbutsa kuchimwa kwao kuja pamene ankapempha Aejipito kuti aŵathandize. Motero Aisraele adzadziŵa kuti Ine ndine Ambuye Chauta.” Pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, chaka cha 27 cha ukapolo, Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, kale Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, idaagwiritsa ntchito ankhondo ake pokathira nkhondo mzinda wa Tiro, mpaka munthu aliyense adachita dazi chifukwa chosenza katundu, ndipo adanyuka pa phewa. Komabe ngakhale iyeyo, kapena gulu lake lankhondo, sadaphulepo kanthu pa ntchito yonse imene adaigwirayo polimbana ndi mzindawo. Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloniyo, ndidzampatsa Ejipito. Adzatenga chuma chake nadzachifunkha nkupita nacho. Zimenezi zidzakhala malipiro a gulu lake lankhondo. Ndampatsa dziko la Ejipito kuti akhale malipiro ake, chifukwa iye ndi ankhondo ake adandigwirira ntchito. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. “Pa nthaŵi imeneyo, Aisraele ndidzaŵapatsa mphamvu zatsopano, ndipo iwe Ezekiele ndidzakulimbitsa kuti udzathe kulankhula pakati pao. Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.” Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, ulose ndipo ulengeze kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: “ ‘Pepani, tsiku latsoka lafika! Ndithudi layandikira, tsiku la Chauta lili pafupi. Tsiku lamitambo, tsiku la kutha kwa mitundu ya anthu. Ku Ejipito kudzafika nkhondo, ndipo ku Etiopiya kudzagwa mavuto. Anthu ambiri adzaphedwa ku Ejipito, chuma chake chidzatengedwa, ndipo maziko ake adzagumuka.’ “Etiopiya, Puti, Ludi, Arabiya yense, Libiya ndiponso anthu a m'dziko logwirizana naye, adzaphedwa nao limodzi pa nkhondoyo. “Zimene ndikunena Ine Chauta ndi izi: Onse othandiza Ejipito adzaphedwa. Ndipo kunyadira mphamvu zake kudzamthera. Anthu ake adzaphedwa pa nkhondo kuyambira ku Migidoli mpaka ku Siyene. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. Dziko la Ejipito lidzasanduka bwinja kupambana mabwinja onse opasuka. Mizinda yake idzakhala yopasuka kupambana mizinda ina yoonongeka. Nditamtentha Ejipito ndi kuthyola onse omuthandiza, adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta. “Nthaŵi imeneyo ikadzafika, amithenga adzapita mofulumira kuchokera kwa Ine kukaopsa Aetiopiya, iwowo osadziŵako kanthu. Ndipo adzada nkhaŵa pa tsiku limene Ejipito adzaonongedwa, chifukwa tsikulo lidzafika ndithu. “Mau a Ine Ambuye Chauta ndi aŵa: Ndidzatuma Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni kuti adzathetse chuma cha Ejipito. Iyeyo ndi anthu ake, mtundu wa anthu ankhalwe kwambiri aja, adzabwera kudzaononga dzikolo. Adzasolola malupanga ao kuti amenyane ndi Aejipito, ndipo dzikolo lidzadzaza ndi mitembo. Ndidzaumitsa mtsinje wa Nailo, ndipo Ejipito ndidzamgulitsa kwa anthu oipa. Dzikolo ndidzaliwononga, pamodzi ndi zonse zam'menemo, polipereka m'manja mwa anthu akudza. Ine Chauta ndatero. “Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ndidzathetsa mafano ndi kuwononga milungu yosema ya ku Memfisi. Sikudzakhalanso mfumu ku Ejipito. Ndipo ndidzaŵaopsa onse okhala m'dziko limenelo. “Mzinda wa Patirosi ndidzausandutsa chipululu. Mzinda wa Zowani ndidzautentha. Mzinda wa Thebesi ndidzaulanga. Mzinda wa Peluziumu, linga lolimba la Ejipito, ndidzauthira mkwiyo wanga, ndipo ndidzaononga gulu lankhondo la ku Thebesi. Ejipito yense ndidzamtentha, ndipo Memfisi adzavutika kwambiri. Malinga a ku Thebesi adzagumuka, ndipo makoma ake adzaonongekeratu. Anyamata a ku Oni ndi a ku Pibeseti adzaphedwa pa nkhondo, ndipo akazi adzatengedwa ukapolo. Ku Tehafinehesi kudzachita mdima, pamene ndidzathyole mphamvu za Ejipito kumeneko. Motero kunyada kwake kudzatha. Mitambo idzamuphimba, ndipo okhala m'midzi yake adzatengedwa ukapolo. Motero ndidzamlanga Ejipito, ndipo adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.” Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri la mwezi woyamba, chaka cha khumi ndi chimodzi cha ukapolo, Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti: “Iwe mwana wa munthu, ndathyola dzanja la Farao, mfumu ya ku Ejipito. Ona, sadalimange kuti lichire, ndipo sadalilimbitse ndi nsalu kuti lithe kugwiranso lupanga. Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndikudana naye Farao, mfumu ya ku Ejipito. Ndidzamthyola manja onse, lamoyo ndi lothyokalo, ndipo lupanga lake lidzamtayika. Ndidzaŵamwaza Aejipito pakati pa mitundu ya anthu ndi kuŵabalalitsira ku maiko ambiri. Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babiloni, ndipo m'manja mwake ndidzaikamo lupanga langa. Koma Farao ndidzamthyola manja, ndipo adzabuula ngati wolasidwa koopsa pamaso pa mfumu ya ku Babiloniyo. Ndithu ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babiloni, koma manja a Farao adzafooka. Motero anthu adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndikadzaika lupanga langa m'manja mwa mfumu ya ku Babiloni. Ndipo adzaligwiritsa ntchito pomenya nkhondo ndi dziko la Ejipito. Ndidzamwaza Aejipito pakati pa mitundu ya anthu, ndi kuŵabalalitsira ku maiko ambiri. Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.” Pa tsiku loyamba la mwezi wachitatu, chaka cha khumi ndi chimodzi cha ukapolo, Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, unene mau aŵa kwa Farao mfumu ya ku Ejipito pamodzi ndi gulu lake la nkhondo: “ ‘Kodi pa ukulu wanu nkukuyerekezani ndi yani? Ndithu ndidzakufanizirani ndi mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni, wa nthambi zabwino zochititsa mthunzi m'nkhalango, nthambi zosomphoka, zofika mpaka ku mitambo. Madzi ndiwo amene ankaukulitsa, ndipo akasupe ankautalikitsa. Mitsinje inkayenda mozungulira kumene unaliri, mifuleni yake inkafika ku mtengo uliwonse m'dzikomo. Koma mtengo uwu udatalika kwambiri kupambana mtengo wina uliwonse. Nthambi zake zidachuluka ndi kutalika kwambiri, popeza kuti mizu yake inkalandira madzi ambiri. Mbalame zamumlengalenga zinkamanga zisa zake m'nthambi za mtengowo. Nyama zonse zakuthengo zinkaswanirana m'munsi mwa nthambizo. Mitundu yonse yotchuka ya anthu inkakhala mumthunzi mwake. Unali mtengo wokongola kwambiri wa nthambi zitalizitali, chifukwa choti mizu yake inkazama ndi kulandira madzi ambiri. M'munda wa Mulungu munalibe mkungudza wofanafana ndi umenewo. Munalibe mtengo wa paini wa nthambi zofanafana ndi zake. Munalibenso mkuyu umene unali ndi nthambi zotere. M'munda wa Mulungu munalibe mtengo wina wofanafana ndi umenewu kukongola kwake. Ndi Ineyo Mulungu amene ndidaukongoletsa, pochulukitsa nthambi zake, kotero kuti mitengo yonse ya mu Edeni, munda wa Mulungu inkachita nawo nsanje.’ “Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Chifukwa choti mtengowo udatalika kwambiri nkufika mpaka ku mitambo, ndipo unkanyada pokula choncho, Ine ndidaupereka m'manja mwa mfumu yolamulira anthu a mitundu ina, kuti mfumuyo iwulange potsata zolakwa zake. Alendo ankhalwe kwambiri pakati pa mitundu ya anthu adzaudula, ndipo adzangoutaya. Nthambi zake zidzagwera pa mapiri, ndiponso m'zigwa zonse. Nthambi zakezo zidzathyokera m'mitsinje yam'dzikomo. Motero anthu a mitundu yonse ya dziko lapansi amene ankasangalala mumthunzi mwake adzausiya nachoka. Mbalame zonse zamumlengalenga zidzakhala pa thunthu la mtengo wakugwawo. Nyama zonse zakuthengo zidzakhala pa nthambi zake. Zonsezi zidzatero kuti pasakhale mtengo ndi umodzi womwe wa m'mbali mwa mtsinje umene udzatalike kwambiri, kapena umene nsonga zake zidzafike ku mitambo. Ndiponso pasadzakhale mitengo ina yolandira bwino madzi, imene msinkhu wake ungafike ku mitambo. Pakuti yonseyo kutha kwake ndi kufa, kupita kunsi kwa dziko lapansi, kukakhala pamodzi ndi anthu akufa, amene adaloŵa kale m'manda. “Zimene Ine Ambuye Chauta ndikunena ndi izi: Mkungudzawo utatsikira ku manda, ndidauza nyanja kuti iwulire maliro pa kuuphimba. Ndidaumitsa mitsinje yake, ndipo madzi ambiri adaphwa. Ndidachititsa mdima pa Lebanoni chifukwa cha mtengowo, ndipo mitengo yonse yam'dzikomo idauma. Mitundu ya anthu idagwedezeka pakumva mkokomo wa kugwa kwake, pamene ndidautsitsira ku manda pamodzi ndi amene adafa. Pamenepo ku dziko la akufa mitengo yonse ya ku Edeni, ndi yonse yokongola ya ku Lebanoni yothiriridwa bwino, idasangalatsidwa chifukwa cha zimenezi. Mitundu imene inkakhala mumthunzi mwake chifukwa cha kumvana nawo, nayonso idapezana nawo kumandako, pamodzi ndi amene adaphedwa ku nkhondo. “Pakati pa mitengo ya ku Edeni, kodi unalipo ndi umodzi womwe wolingana nawe pa ulemerero ndi pa ukulu? Komabe iwenso udzatsikira ku dziko la akufa, pamodzi ndi mitengo ina yonse ya ku Edeni. Udzagona pamodzi ndi amene adaphedwa ku nkhondo, m'gulu la anthu osaumbalidwa! Mtengowo ndi mfumu ya ku Ejipito pamodzi ndi anthu ake. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.” Pa tsiku loyamba la mwezi wa khumi ndi chiŵiri, chaka cha khumi ndi chiŵiri cha ukapolo, Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, imbira Farao, mfumu ya ku Ejipito, nyimbo yamaliro. Umuuze uthenga uwu wakuti: “Iwe umadziyesa mkango pakati pa mitundu ya anthu, koma uli ngati ng'ona. Umakhuvula m'mitsinje yako. Umavonongera madzi ndi mapazi ako, ndi kudetserera mitsinje. Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndikadzasonkhanitsa pamodzi anthu a mitundu yambiri, ndidzakuponyera khoka ndipo iwowo adzakugwira m'kombe mwanga. Ndidzakuponya ku mtunda ndi kukutaya pansi. Ndidzabweretsa mbalame zamumlengalenga kuti zidzatere pa iwe, ndiponso zilombo za m'dziko lonse kuti zidzakudye. Nyama yako ndidzaiyanika pa mapiri, ndipo zigwa zidzadzaza ndi zotsala zako. Ndidzanyowetsa dziko ndi magazi ako, mpaka ku mapiri komwe, ndipo mitsinje idzadzaza ndi nyama yako. Ndikadzakuwononga, ndidzaphimba thambo, ndipo ndidzadetsa nyenyezi. Ndidzaphimba dzuŵa ndi mtambo, ndipo mwezi sudzaŵala. Ndidzazimitsa zoŵala zonse zamumlengalenga, ndipo dziko lako ndidzalichititsa mdima. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. “Ndidzavutitsa mitima ya anthu a mitundu yambiri, pamene ndidzakupititsa ku ukapolo pakati pa mitundu ina, ku maiko amene sudaŵadziŵe. Ndidzadabwitsa anthu ambiri ndi zimene zidzakugwere. Mafumu ao adzanjenjemera pokumbukira iwe, nditaŵaonetsa lupanga langa. Pa tsiku la kugwa kwako, aliyense adzadera nkhaŵa moyo wake. “Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Nkhondo ya mfumu ya ku Babiloni idzakufika. Ndidzagwetsa gulu lako lonse lankhondo ndi malupanga a asilikali oopsa kwambiri kupambana a mitundu ina yonse. “Adzathetsa kunyada kwa Ejipito, ndipo gulu lake lonse lankhondo lidzaonongeka. Ndidzaononga ziŵeto zao zonse zokhala pambali pa madzi am'dzikomo. Kumadziko sikudzaonekanso phazi la munthu, ndipo phazi la nyama silidzavonongeranso madzi. Pambuyo pake ndidzayeretsa madzi akumeneko, ndipo mitsinje idzayenda mokometsera ngati mafuta. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. Ejipito nditamsandutsa bwinja, ndipo dziko lonse nditaliwononga, nditapha onse okhala kumeneko, adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta. “Mau angaŵa adzakhala nyimbo yamaliro, ndipo akazi a mitundu yachilendo adzaiimba, kuimbira Ejipito ndi gulu lake lonse lankhondo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.” Pa tsiku la khumi ndi chisanu la mwezi woyamba, chaka cha khumi ndi chiŵiri cha ukapolo, Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, lira kwambiri chifukwa cha anthu ochuluka a ku Ejipito, ndipo uŵaloŵetse, pamodzi ndi anthu a m'maiko ena amphamvu, ku dziko la anthu akufa. Uŵafunse kuti, ‘Kani ndinu okongola kupambana ena? Tsikirani ku manda pamodzi ndi ena onse osaumbalidwa.’ Aejipito adzagwa pakati pa anthu amene adaphedwa pa nkhondo. Lupanga nlosololasolola, iwowo adzaphedwa pamodzi ndi anthu ao ochuluka. M'kati mwa manda atsogoleri amphamvu pamodzi ndi ogwirizana nawo azidzakambirana kuti, ‘Kani anthu osaumbalidwa aja, ophedwa pa nkhondo, afika kunsi kuno. Si aŵa agona apaŵa!’ “Komweko kuli Asiriya ndipo ankhondo ake onse ali m'manda omzungulira. Onsewo adaphedwa pa nkhondo. Manda ao ali m'malo ozama kwambiri m'dziko la anthu akufa, ndipo manda ao adazungulira manda ake. Iwowo kale ankaopsa m'dziko la anthu amoyo, koma tsopano onsewo adafa, adaphedwa pa nkhondo. “Komweko kulinso Elamu ndipo ankhondo ake onse ali m'manda omzungulira. Onsewo adaphedwa pa nkhondo. Anthuwo adatsikira ku manda ali osaumbalidwa. Iwowo kale ankaopsa m'dziko la anthu amoyo. Tsopano akuchita manyazi, pamodzi ndi amene ali m'manda. Elamuyo amupangira malo ogonapo pakati pa anthu ophedwa, pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo, loikidwa momzungulira. Onsewo ndi osaumbalidwa, ophedwa pa nkhondo. Zoonadi, anthu amene kale ankaopsa m'dziko la anthu amoyo, tsopano akuchita manyazi pamodzi ndi amene ali m'dziko la anthu akufa. Aikidwa pakati pa anthu ophedwa. “Komwekonso kuli Meseki ndi Tubala. Ankhondo ao onse ali m'manda oŵazungulira. Anthuwo ndi osaumbalidwa, ndipo adaphedwa pa nkhondo. Iwowo kale ankaopsa m'dziko la anthu amoyo. Sadaikidwe mwaulemu ngati ankhondo amphamvu amakedzana, amene adatsikira ku dziko la anthu akufa ndi zida zao zomwe zankhondo. Malupanga ao adaŵaika ku mitu yao, ndipo zishango zao adaphimbira mafupa ao. Kale anthu amphamvu ameneŵa ankaopsa m'dziko la anthu amoyo. “Iwenso Farao, udzatswanyika ndipo udzagona pamodzi ndi anthu akufa osaumbalidwa, pamodzi ndi amene adaphedwa pa nkhondo. Komweko kuli Edomu pamodzi ndi mafumu ake ndi akalonga ake onse. Ngakhale anali amphamvu, komabe adaikidwa m'manda. Akugona pamodzi ndi anthu osaumbalidwa, pamodzi ndi onse amene adatsikira ku dziko la anthu akufa. “Komweko kulinso akalonga onse akumpoto, pamodzi ndi anthu onse a ku Sidoni, amene adatsikira ku dziko la anthu akufa mwamanyazi, pamodzi ndi ophedwa, ngakhale anali oopsa ndi mphamvu zao. Akugona osaumbalidwa pamodzi ndi ophedwa pa nkhondo. Kumeneko akuchita manyazi pamodzi ndi onse amene adatsikira kale ku dziko la anthu akufa. “Farao akadzaona onseŵa, iye ndi magulu ake ankhondo adzathuza mtima pokumbukira kuchuluka kwa anthu ake amene adaphedwa pa nkhondo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. Ndithudi ankaopsa m'dziko la anthu amoyo, koma iyeyo ndi magulu ake onse ankhondo adzaikidwa pamodzi ndi osaumbalidwa, pamodzi ndi onse ophedwa pa nkhondo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.” Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, uza anthu a mtundu wako zimene zimachitika ndikatumiza nkhondo m'dziko. Suja anthu am'dzikomo amasankha mmodzi pakati pao kuti akhale mlonda. Iye akaona mdani akubwera, amaliza lipenga kuti achenjeze aliyense. Wina akalimva lipengalo, koma osasamala, ndipo mdani akabwera nkumupha, wadziphetsa ndi mtima wake. Wadziphetsa yekha chifukwa choti sadasamale chenjezo. Akadasamala, akadapulumuka. Koma mlonda akaona mdani akubwera, iye osaliza lipenga kuti achenjeze anthu, tsono mdani nkubwera napha munthu wina, ngakhale kuti munthuyo wafera machimo ake, Ine ndidzamzenga mlandu mlonda uja chifukwa cha imfa ya mnzakeyo. “Tsono iwe mwana wa munthu, ndakuika kuti ukhale mlonda wa Aisraele. Ukamva mau anga, uŵachenjeze. Ndikauza munthu woipa kuti, ‘Munthu woipa iwe, udzafa,’ iwe nupanda kumchenjeza kuti aleke makhalidwe oipa, kuti akhalebe ndi moyo, munthuyo adzafadi ali wochimwa, koma iweyo ndidzakuzenga mlandu chifukwa cha imfa yake. Koma munthu woipa ukamchenjeza kuti asiye njira zake zoipa, iye nkupitiriza makhalidwe ake oipawo, adzafa ali wochimwa, koma iweyo udzapulumutsa moyo wako. “Iwe mwana wa munthu, uŵakumbutse Aisraele mau ao akuti, ‘Talemedwa ndi machimo athu ndipo tikuwonda nazo zolakwa zimene tachita. Kodi tingakhale ndi moyo bwanji?’ Uŵauze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndithudi, pali Ine ndemwe, sindikondwa ndikaona munthu woipa alikufa. Ndikadakonda kuti aleke kuchimwako kuti akhale ndi moyo. Inu Aisraele, muferanji? Tembenukani, lekani zoipa zimene mukuchita. “Tsono iwe mwana wa munthu, uza anthu ako kuti, Pamene munthu wochita chifuniro cha Mulungu achimwa, zabwino zimene adaachita sizidzampulumutsa. Woipa akaleka kuchimwa, sadzalangidwa. Ndipo munthu wochita chifuniro cha Mulungu akayamba kuchimwa, sadzatha kukhala ndi moyo chifukwa cha ntchito zake zabwino. Ngakhale ndiwuze munthu wochita chifuniro cha Mulungu kuti adzakhala ndi moyo, ngati iye agonera pa zabwino zimene adaachita kale, nayamba kuchimwa, zabwino zake zonse zimene adaachitazo zidzaiŵalika. Adzafera zochimwa zakezo. Chimodzimodzi ndikamchenjeza munthu wochimwa kuti adzafa, tsono iye nkuleka kuchimwako, namachita zolungama ndi zabwino, monga kubweza chigwiriro chimene adatenga chifukwa cha ngongole, kubweza zimene adaba, kusiya zochimwa ndi kumasunga malamulo opatsa moyo, ndithu sadzafa, adzakhala ndi moyo. Ndidzamkhululukira machimo ake amene adaachita. Chifukwa cha zabwino ndi zolungama zimene adachitazo, ndithu adzakhala ndi moyo. “Komabe anthu a mtundu wako amati, ‘Zimene Chauta amachitazi nzopanda chilungamo.’ Iyai, koma makhalidwe ao ndiwo amene ali osalungama. Munthu wabwino akaleka kuchita zabwino, nayamba kumachita zoipa, adzafa nazo. Munthunso woipa, akaleka kuchimwa, namachita zolungama ndi zabwino, adzapulumutsa moyo wake. Tsono inu am'banja la Israele, mumanena kuti, ‘Zimene Chauta amachitazi nzopanda chilungamo.’ Iyai, aliyense mwa inu Ine ndidzamuweruza potsata zochita zake.” Pa tsiku lachisanu la mwezi wakhumi, chaka cha khumi ndi chiŵiri cha ukapolo wathu, munthu amene adapulumuka ku Yerusalemu, adabwera kudzandiwuza kuti mzinda wagwa. Madzulo, iyeyo asanabwere, ndidaagwidwa ndi mphamvu za Chauta. Koma m'maŵa mwake, munthuyo atafika, Chauta adandibwezera mphamvu zolankhulira, ndipo sindinalinso bububu. Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, anthu amene akukhala m'mizinda yamabwinja ku dziko la Israele, akunena kuti, ‘Abrahamu anali munthu mmodzi yekha, ndipo adamupatsa dziko lonse. Koma ife tilipo ambiri, motero tsopano dzikolo ndi lathu.’ Tsono uŵauze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, ‘Mumadya nyama pamodzi ndi magazi omwe. Mumapembedza mafano, mumapha anthu. Kodi tsono dzikolo nkudzakhaladi lanu?’ Mumadalira malupanga anu. Mumachita zonyansa, ndipo aliyense amachita chigololo ndi mkazi wa mnzake. Kodi dzikolo nkudzakhaladi lanu? Uŵauze kuti, Ine Ambuye Chauta ndikuti, Pali ine ndemwe wamoyo, anthu amene adatsala m'mizinda yamabwinja, adzaphedwa ndi lupanga. Amene adatsala m'midzi, ndidzaŵapereka ku zilombo kuti ziŵadye. Amene adabisala m'mapiri ndi m'mapanga, adzafa ndi mliri. Dzikolo ndidzalisandutsa tsala ndiponso chipululu. Mphamvu zimene ankanyada nazo zidzatheratu. Mapiri a ku Israele adzasanduka thengo, kotero kuti munthu sadzadutsako. Ndikadzalanga anthu chifukwa cha zonyansa zimene adachita, ndi kusandutsa dzikolo kuti likhale tsala ndiponso chipululu, pamenepo adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta. “Koma kunena za iwe, mwana wa munthu, anthu a mtundu wako amalankhula za iwe, akamakumana pafupi ndi makoma a mzinda ndi pa makomo a nyumba zao. Amauzana kuti, ‘Tiyeni tsopano tikamve zimene Chauta wanena.’ Anthu anga amadzasonkhana kwa iwe nakhala pansi kuti amve zimene iweyo unene. Koma akazimva, sazitsata zimenezo. Zokamba zao zimaonetsa chikondi, m'menemo mitima yao imangokonda phindu chabe. Kwa iwowo sindiwe kanthu konse, ndiwe munthu wamba chabe womangoimba nyimbo zachikondi ndi liwu lokoma poimba zeze. Kumva amamva mau ako onse, koma saŵagwiritsa ntchito. Koma zimene wanena zikadzachitikadi—ndipo zidzachitika kumene—apo adzadziŵa kuti pakati pao panalidi mneneri.” Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, ulengeze mau oimba mlandu abusa a Israele. Ulengeze, uŵauze kuti ‘Zimene akunena Ambuye Chauta ndi izi: Tsoka kwa inu abusa a ku Israele, amene mumangodzisamala inu nokha. Kodi suja abusa amayenera kusamala nkhosa? Chambiko mumadya, zaubweya mumavala, ndipo nyama zonenepa mumapha, koma nkhosa osasamala konse. Nkhosa zofooka simudazilimbikitse, zodwala simudazichiritse, zopweteka simudazimange mabala ake, zosokera simudazibweze, ndipo zotayika simudazifunefune. Koma munkaziŵeta mozunza ndi mwankhalwe. Ndiye zinkangoti balalabalala, poti panalibe mbusa. Motero zidasanduka chakudya cha zilombo zonse zakuthengo. Nkhosa zanga zidamwazikana nkumangoyendayenda ku mapiri ndi ku magomo ataliatali. Zidabalalikira m'dziko lonse popanda wina wozilondola kapena kuzifunafuna.’ “Tsono abusa inu, tamverani zimene Ine Chauta ndikukuuzani: Pali ine ndemwe, nkhosa zanga zidajiwa ndi zilombo zakuthengo, zidasanduka chakudya cha zilombo chifukwa chosoŵa abusa. Abusa anga sadalondole nkhosa zanga, ankangosamala za iwo okha, osasamala nkhosa. Nchifukwa chake abusa inu, imvani mau a Ine Chauta. Ndikuti, Ndaipidwa nanu abusanu. Ndidzakulandani nkhosa zanga, simudzazidyetsanso. Ndidzakuchotsani pa ntchito yaubusa, kuti musadzasamalenso za inu nokha. Ndidzapulumutsa nkhosa zanga kukamwa kwanu, ndipo simudzazidyanso. “Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi, Tsopano nkhosa zangazo ndidzazifunafuna ndekha mwiniwakene, ndipo ndidzazisamala. Monga mbusa amanka nafunafuna nkhosa zake, pamene zina zabalalikira kutali, Inenso ndidzatero, kunka ndikufunafuna nkhosa zanga. Ndidzazipulumutsa konse kumene zidamwazikira pa nthaŵi yamdima ndi yankhungu. Ndidzazitulutsa pakati pa mitundu yonse ya anthu, ndidzazisonkhanitsa kuchokera ku maiko ena, ndipo ndidzazibwezera ku dziko lakwao. Ndidzaziŵetera ku mapiri a ku Israele, pafupi ndi mitsinje yake, ndi ku malo onse abwino kumene anthu amakhalako. Ndidzaziŵetera ku mabusa abwino, ndipo zizidzadya msipu wonenepetsa ku mapiri okwera a Israele. Kumeneko zidzapumula ku mabusa abwino amsipu. Zidzapezadi mabusa abwino ku mapiri a Israele. Ineyo mwiniwake ndidzakhala mbusa wa nkhosa zanga. Ndipo Ine ndemwe ndizidzazipumulitsa. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. Zotayika ndidzazifunafuna, zosokera ndidzazibweza, zopweteka ndidzazimanga mabala ake. Zofooka ndidzazilimbikitsa, koma zonenepa ndi zamphamvu ndidzaziwononga. Ndidzaŵeta nkhosa zanga mwachilungamo.” “Tsono kunena za inu, nkhosa zanganu, Ine Ambuye Chauta ndikukuuzani kuti, Ndidzaweruza pakati pa nkhosa ndi nkhosa, pakati pa nkhosa zamphongo ndi atonde. Kodi inu simukhutira kudya pa busa labwino? Nanga mumaponderezeranji zimene simudya? Kodi simukhutira kumwa madzi abwino? Nanga madzi amene simumwa mumaŵadetsereranji ndi mapazi anu? Kodi mukufuna kuti nkhosa zanga zizidya udzu umene mudaponderezawo, ndi kumamwa madzi amene mudadetserera? “Tsono Ine Ambuye Chauta ndikukuuzani kuti, Ineyo mwiniwake ndidzaweruza ndekha pakati pa inu nkhosa zonenepanu ndi zinzanu zoondazo. Zofooka mumaziwomba ndi kuzikankhira kumbali, ndipo mumazigunda ndi nyanga zanu nkuzimwazira kutali. Koma ndidzazipulumutsa nkhosa zangazo, ndipo sindidzalolanso kuti zijiwe. Ndidzaweruza pakati pa nkhosa ina ndi nkhosa inanso. Ndidzaziikira mbusa mmodzi, mtumiki wanga Davide. Iyeyo ndiye azidzazisamala, ndipo adzakhala mbusa wake. Pamenepo Ine Chauta ndidzakhala Mulungu wake, ndipo mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu yake. Ndatero Ineyo Chauta.” “Ndidzapangana nazo chipangano chamtendere. Zilombo zonse zolusa ndidzazichotsa m'dziko, kuti nkhosa zanga zizidzakhala mwamtendere, ngakhale m'chipululu kapena m'thengo. Ndidzakhazika anthu anga kufupi ndi phiri langa, ndipo ndidzaŵagwetsera mvula pa nthaŵi yake, mvula yake ya madalitso. Mitengo ya m'minda idzabereka zipatso, ndipo minda idzakhala ndi zokolola zake, tsono anthu adzakhala mwamtendere m'dziko lao. Adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, pamene ndidzathyole magoli ao ndi kuŵapulumutsa kwa amene adaŵagwira ukapolo. Anthu a mitundu ina sadzaŵafunkhanso, ndipo zilombo zakuthengo sizidzaŵadya. Adzakhala mwamtendere popanda wina woŵaopsa. Ndidzachulukitsa zolima zao, mwakuti sadzafanso ndi njala m'dzikomo, ndipo choncho anthu a mitundu ina sadzaŵanyozanso. Motero adzadziŵa kuti Ine Chauta Mulungu wao ndili nawo, ndipo kuti iwowo, Aisraelewo, ndi anthu anga. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. ‘Inu ndinu nkhosa zanga, nkhosa zimene ndimadyetsa, ndipo Ine ndine Mulungu wanu. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.’ ” Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, yang'ana ku dziko lamapiri la ku Seiri, ndipo ulengeze mau oliimba mlandu. Anthu akumeneko uŵauze kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: “Inu anthu a ku mapiri a ku Seiri ndikudana nanu. Ndidzakumenyani ndi dzanja langa, ndidzasandutsa dziko lanu tsala ndi chipululu. Mizinda yanu ndidzaisandutsa mabwinja, ndipo dziko lanu lidzakhala chipululu. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta. “Munali adani a Israele nthaŵi zonse, ndipo munkalola kuti anthu ake aziphedwa pa nthaŵi ya mavuto ao, pa nthaŵi imene chilango chao chidafika pa chimake. Tsono Ine Ambuye Chauta ndikuti, ‘Pali Ine ndemwe, ndidzakhetsa magazi anu, ndipo imfa idzakulondolani. Zoonadi, mudakhetsa magazi, tsono imfa idzakulondolani. Phiri la Seiri ndidzalisandutsa tsala ndi chipululu. Ndidzapha onse amene amayenda kumeneko. Mapiri ake ndi zigwa zake ndidzazidzaza ndi mitembo, tsono ophedwa pa nkhondo adzangoti vuu pa magomo, m'zigwa ndi m'mitsinje yanu. Dziko lanu ndidzalisandutsa bwinja mpaka muyaya, ndipo m'mizinda mwanu simudzakhalanso munthu. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.’ “Inu mudanena kuti, ‘Mitundu iŵiri ya anthu, Yuda ndi Israele, idzakhala yathu pamodzi ndi maiko ao omwe.’ Mudatero ngakhale kuti Ine Chauta ndinali nao m'menemo. Tsono Ine Ambuye Mulungu ndikuti, Pali Ine ndemwe, ndidzakuchitani zomwe mudaŵachita anthu anga poŵaonetsa mkwiyo wanu, nsanje yanu ndi chidani chanu. Mudzandidziŵadi pakati panupo, ndikadzakulangani. Mudzadziŵa kuti Ine Chauta ndidamva mau anu onse onyoza mapiri a ku Israele. Mudanena kuti, ‘Mapiri a ku Israele asiyidwa, ndipo atipatsa kuti tiŵaononge.’ Ndidamva zondinyoza zimene mudanena monyada. Ndidadzimvera ndekha zonse! Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ndidzakusandutsani bwinja kotheratu, kotero kuti dziko lonse lapansi lidzakondwa nako kugwa kwanu. Monga momwe inu mudakondwera ndi kugwa kwa Israele, Ine ndidzakuchitaninso zomwezo. Iwe phiri la Seiri, ndi dziko lonse la Edomu, udzasanduka bwinja. Motero anthu onse adzadziŵa kuti Ine ndine Ambuye Mulungu.” Chauta adandiwuza kuti, “Tsono iwe mwana wa munthu, ulalikire mapiri a ku Israele, unene kuti, Inu mapiri a ku Israele, imvani uthenga uwu wochokera kwa Ambuye Chauta: Paja adani anu adanena kuti, ‘Ha, tsopano dziko lamapiri lakale lija lasanduka lathu.’ Ndiye tsono iwe ulengeze ndi kuŵauza kuti ‘Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Pamene adani anu adakusandutsani chipululu ndi kukuponderezani ku mbali zonse, mpaka inu kukhala m'manja mwa anthu a mitundu ina yonse, anthu ankakunenani ndi kukujedani. Nchifukwa chake inu, mapiri a ku Israele, imvani zimene Ine Ambuye Chauta ndikuuza mapiri ndi magomo, zigwembe ndi zigwa, mabwinja ndi mizinda yosiyidwa imene akhala akuifunkha ndi kuinyoza anthu a mitundu yokuzungulirani.’ ” “Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndakhala ndikulankhula ndili ndi mkwiyo woopsa, kuŵaimba mlandu anthu a mitundu ina yonse, makamaka a ku Edomu. Iwoŵa, mwa chimwemwe chodzaza tsaya ndiponso monyoza, adalanda dziko langa kulisandutsa lao, ndi kutengeratu mabusa ake.” “Nchifukwa chake ulengeze za dziko la Israele, ndipo uuze mapiri ndi magomo, zigwembe ndi zigwa, mau a Ine Ambuye Chauta, akuti, Ndikulankhula ndi mtima wokwiya kwambiri, chifukwa chakuti mudapirira manyozo ochokera kwa mitundu ina ya anthu. Motero ndalumbira ndithu kuti anthu a mitundu yokuzunguliraniyo nawonso adzamva manyozo. Koma inu, mapiri a ku Israele, mudzaphukanso nthambi, ndipo anthu anga Aisraele mudzaŵabalira zipatso, poti ali pafupi kubwerera kwao. Ine ndikusamala za inu, ndipo ndidzakukomerani mtima. Mudzalimidwanso ndi kubzalidwa. Ndidzachulukitsa anthu mwa inu ndiponso m'dziko lonse la Israele. M'mizinda mudzakhalanso anthu, ndipo nyumba zonse zimene zidaali mabwinja zidzamangidwanso. Ndidzachulukitsa anthu anu pamodzi ndi nyama zomwe. Adzachuluka ndithu ndipo adzabereka ana ambiri. Anthu okhala mwa inu ndidzaŵachulukitsa monga momwe adaliri kale, ndipo ndidzakuchitirani zabwino kuposa kale. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta. Ndidzalola kuti anthu ayende pa inu, ndiye kuti inuyo anthu anga Aisraele. Iwowo adzakhazikika pa inu, ndipo inuyo mudzakhala chuma chao. Simudzalandanso ana a mtundu wao.” “Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Anthu ena amanena kuti iwe ndiwe dziko lodya anthu ake, ndiponso lolanda ana a anthu a mtundu wake. Sudzadyanso anthu, kapena kulanda ana a mtundu wako. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. Sindidzakulolanso kuti umve manyozo a anthu a mitundu ina, kapena kupirira kunyodola kwao, ndipo sudzaphunthwitsanso anthu a m'dziko lako. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.” Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Munthu iwe, pamene Aisraele ankakhala m'dziko lao, adaliipitsa ndi makhalidwe oipa ndiponso ndi zochita zao. Ndidaona kuti makhalidwe ao anali onyansa pa za chipembedzo, ngati mkazi amene ali kunthaŵi yake. Ndidaŵalanga mokalipa chifukwa cha magazi a anthu amene iwo adakhetsa m'dzikomo, ndiponso chifukwa cha mafano amene iwo adaipitsa nawo dzikolo. Ndidaŵamwaza pakati pa anthu a mitundu ina, ndipo ndidaŵabalalitsira ku maiko osiyanasiyana. Ndidaŵalanga potsata makhalidwe ao ndi ntchito zao. Atafika pakati pa anthu a mitundu inayo, kulikonse kumene ankapita, adaipitsa dzina langa loyera. Zidatero chifukwa anthu ponena za iwowo ankati, ‘Aŵa ndi anthu a Chauta, koma onani adachotsedwa ku dziko lake.’ Komabe Ineyo ndinkadera nkhaŵa dzina langa loyera, limene Aisraele adaliipitsa pamene ankakhala pakati pa anthu a mitundu ina kumene adapita.” “Nchifukwa chake Aisraelewo uŵauze kuti Ine Ambuye Chauta mau anga ndi aŵa: Zimene nditi ndichite, sindichita chifukwa cha inuyo Aisraelenu ai, koma chifukwa cha dzina langa loyera limene mudaliipitsa pakati pa anthu a mitundu ina kumene mudapita. Dzina langa lotchuka limene lakhala lonyozeka pakati pa anthu a mitundu ina, ndidzaonetsa kuti nloyera. Tsono anthu a mitundu inayo atazindikira kuti ndaonetsa kuyera kwa dzina langa mwa inu, adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. Ndidzakutulutsani pakati pa mitundu inayo, ndidzakusonkhanitsani kuchokera ku dziko lililonse, ndipo ndidzakubwezani ku dziko lanu. Ndidzakuwazani madzi angwiro, ndipo mudzayera, zonse zokuipitsani zidzachoka. Ndiponso ndidzakuyeretsani pochotsa mafano anu onse. Ndidzakupatsani mtima watsopano ndi kuloŵetsa mzimu watsopano mwa inu. Ndidzakuchotserani mtima wanu wouma ngati mwalawo ndi kukupatsani mtima wofeŵa ngati mnofu. Ndidzaika mzimu wanga mwa inu, ndipo ndidzakutsatitsani malangizo anga, ndi kukusungitsani malamulo anga mosamala kwambiri. Mudzakhala m'dziko limene ndidapatsa makolo anu. Inu mudzakhala anthu anga, Ine ndidzakhala Mulungu wanu. Ndidzakupulumutsani ku zonse zokuipitsani. Ndidzakuchulukitsirani tirigu, ndipo sindidzakugwetseraninso njala. Ndidzabereketsa mitengo zipatso zambiri ndipo nthaka idzabala zokolola zambiri, kotero kuti simudzanyozekanso chifukwa cha njala pakati pa anthu a mitundu ina. Apo mudzakumbukira makhalidwe anu oipa ndi ntchito zanu zoipa. Mudzachita manyazi chifukwa cha machimo anu ndi zonyansa zimene mudachita. Ndiyetu dziŵani kuti sindidzachita zimenezi chifukwa cha inuyo ai. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. Choncho Aisraele inu, chitani manyazi, ndipo mugwetse nkhope chifukwa cha makhalidwe anu oipa. “Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Pamene ndidzachotsa machimo anu, ndidzaikamonso anthu m'mizindamo, ndipo ndidzamanganso nyumba pa mabwinja aja. Dziko limene lidaasanduka tsala, anthu azidzalimamonso. Kale aliyense wopita m'njira ankaliwona ngati chipululu, tsopano adzaona kuti nlolimidwa. Motero anthu azidzati, ‘Dziko lija lidaali tsalali lasanduka ngati munda wa Edeni. Tsopano mukukhala anthu m'mizinda imene kale idaali mabwinja yosiyidwa ndi yoonongeka. Ndiponso mizindayo tsopano ili ndi malinga olimba.’ Anthu a mitundu ina amene adatsala pafupi nanu, adzadziŵa kuti Ineyo Chauta ndi amene ndidamanganso mizinda yoonongeka ndi kubzalanso zinthu zatsopano m'dziko losiyidwalo. Ineyo Chauta ndalankhula zimenezi, ndipo ndidzazichitadi. “Ine Ambuye Chauta mau anga ndi aŵa: Ndidzaŵalolanso Aisraele kuti andipemphe zimene afuna kuti ndiŵachitire. Ndidzachulukitsa anthu ao ngati nkhosa. Adzachuluka ngati nkhosa za ku Yerusalemu zimene ankazipereka kale ku nsembe pa nthaŵi ya chikondwerero. Motero mizinda yao yamabwinja ija idzadzazadi ndi magulu a anthu, ndipo iwowo adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.” Mphamvu ya Chauta idandigwira, Mzimu wa Chauta udandinyamula nkukandikhazika pakati pa chigwa. Chigwacho chinali chodzaza ndi mafupa. Chauta adandiyendetsa uku ndi uku pakati pa mafupawo. Mafupawo analitu ochuluka kwambiri m'chigwa chonsecho, ndipo anali ochita kuti gwaa kuuma kwake. Tsono adandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi mafupa ameneŵa angathe kukhalanso ndi moyo?” Ine ndidati, “Ambuye Chauta, ndi Inuyo amene mukudziŵa zimenezi.” Apo adandiwuza kuti, “Alalikire mafupa ameneŵa, uŵauze mafupa oumawo kuti amve mau a Ine Chauta. Unene kuti zimene Ine Ambuye Chauta ndikuŵauza mafupawo ndi izi: Ndidzauzira mpweya mwa inu, ndipo mudzakhalanso ndi moyo. Ndidzakupatsani mitsempha ndi mnofu, nkukukutani ndi khungu. Ndidzauzira mpweya mwa inu, ndipo mudzakhalanso ndi moyo. Tsono mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.” Pamenepo ndidayamba kulalika monga momwe adandilamulira. Ndikulalika choncho ndidangomva kuti gogobedegogobede! Mafupa aja kuyamba kulumikizana. Ine ndiyang'ane, ndidaona kuti pali mitsempha, kenaka mnofu ukuwonekanso, potsiriza nkubwera khungu pamwamba pake, koma munalibe mpweya mwa iwo. Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, ulalike ndi kuuza mpweya mau a Ine Ambuye Chauta, akuti, ‘Mpweya iwe, bwera kuno, bwera kuchokera ku mphepo zinai, dzaŵauzire anthu ophedwaŵa, kuti akhalenso ndi moyo.’ ” Motero ndidayamba kulalika monga adandilamulira. Tsono mpweya udaloŵa mwa iwo, ndipo akufa aja adakhala ndi moyo, naimirira. Linali gulu lalikulu kwambiri la ankhondo. Kenaka Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, mafupa ameneŵa ndi Aisraele onse. Iwo amanena kuti, ‘Mafupa athu ndi ouma, chiyembekezo chathu chidataika, taonongekeratu.’ Nchifukwa chake uŵalalikire ndi kuŵauza kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Inu anthu anga, ndidzafukula manda anu, ndipo ndidzakutulutsanimo. Ndidzakubwezerani ku dziko la Israele. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndikadzafukula manda anu ndi kukutulutsanimo, inu anthu anga. Tsono ndidzaika mzimu wanga mwa inu ndipo mudzakhalanso ndi moyo, pambuyo pake ndidzakukhazikani m'dziko lanu. Choncho mudzadziŵa kuti Ine Chauta ndalankhula zimenezi, ndipo ndidzazichitadi. Ndikutero Ine Chauta.” Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, tenga ndodo, ulembepo kuti, ‘Ya Ayuda ndi Aisraele ogwirizana nawo.’ Tsono utenge ndodo ina, ulembepo kuti, ‘Ya Aefuremu, ndiye kuti fuko la Yosefe, ndi Aisraele ogwirizana nawo.’ Tsono utenge ndodo ziŵirizo ndi kuzilumikiza kuti zikhale ngati ndodo imodzi. Anthu akwanu akakufunsa tanthauzo lake la zimenezi, uŵauze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndili pafupi kutenga ndodo ya Yosefe, imene ili m'manja mwa Efuremu, pamodzi ndi Aisraele ogwirizana nawo, ndiilumikiza ndi ndodo ya Yuda kuti zikhale ndodo imodzi. Ndipo zidzakhaladi imodzi m'manja mwanga. Ndodo zimene ukulembapozo zikadzakhala m'manja mwako, pamaso pa anthu onse, pamenepo udzaŵauze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndidzaŵaitana Aisraele kuchokera ku malo ao aukapolo pakati pa anthu a mitundu ina. Ndidzaŵasonkhanitsa kuchokera ku mphepo zinai ndi kuŵabwezera ku dziko lao. Ndidzaŵasandutsa mtundu umodzi m'dzikomo, ku mapiri a Israele, ndipo adzakhala ndi mfumu imodzi yokha. Sadzakhalanso mitundu iŵiri ya anthu kapena kugaŵikana maufumu aŵiri. Sadzadziipitsanso ndi mafano ao ndi zinthu zina zonyansa, kapena ndi zochimwa zao zina zilizonse. Ndidzaŵapulumutsa ku machimo ao onse, ndipo ndidzaŵayeretsa. Motero iwowo adzakhala anthu anga, ndipo Ineyo ndidzakhala Mulungu wao. “Mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu yao, motero onsewo adzakhala ndi mbusa mmodzi. Adzatsata malamulo anga, adzamvera mosamala malangizo anga. Adzakhala m'dziko limene ndidapatsa mtumiki wanga Yakobe, kumene ankakhala makolo anu. Iwowo, pamodzi ndi ana ao ndi zidzukulu zao, adzakhala kumeneko mpaka muyaya. Ndipo mtumiki wanga Davide adzakhala mtsogoleri wao mpaka muyaya. Ndidzachita nawo chipangano chamtendere. Chipangano chimenechi chidzakhala chao mpaka muyaya. Ndidzaŵakhazikitsa ndi kuŵachulukitsa, ndipo ndidzaika Nyumba yanga pakati pao mpaka muyaya. Nyumba yanga idzakhala pakati pao. Ineyo ndidzakhala Mulungu wao, ndipo iwowo adzakhala anthu anga. Apo anthu a mitundu ina adzadziŵa kuti Ine Chauta Aisraele ndimaŵasandutsa oyera, chifukwa chakuti Nyumba yanga ili pakati pao mpaka muyaya.” Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, udzudzule Gogi, wa ku dziko la Magogi, kalonga wamkulu wa mzinda wa Meseki ndi wa Tubala, ndipo umuimbe mlandu. Umuuze kuti Ine Ambuye Chauta, ndikuti, Ndikudana nawe, iwe Gogi, kalonga wamkulu wa ku Meseki ndi ku Tubala. Ndidzakuzunguza, ndidzakukola ndi mbedza m'kamwa mwako. Ndidzakutulutsira poyera, iweyo pamodzi ndi gulu lako lonse lankhondo, akavalo ndi okwerapo ake. Onsewo adzakhala atanyamula zishango ndi malihawo, malupanga ao ali osololasolola. Pamodzi ndi iwowo palinso asilikali a ku Persiya, ku Etiopiya ndi ku Puti. Onsewo ali ndi zishango ndi zisoti zankhondo. Palinso Gomeri ndi magulu ake onse ankhondo, banja la Togarima ndi gulu lake lankhondo lochokera kutali kumpoto. Palidi mitundu ya anthu ambiri imene ili nawe. “Konzekani, mukhale okonzeka ndithu, iweyo pamodzi ndi gulu lonse lankhondo limene lasonkhana mokuzungulira. Ndiwe amene udzaŵatsogolere pokamenya nkhondo. Ndidzakuitana patapita masiku ambiri. Zaka zikubwerazi, ndidzakuloŵetsa m'dziko lopulumuka ku nkhondo. Udzaŵapeza anthu atasonkhana kuchokera ku mitundu yambiri ya anthu, atakhazikika ku mapiri a Aisraele amene adaasiyidwa nthaŵi yaitali. Aisraelewo adaŵatulutsa pakati pa mitundu ya anthu, ndipo onsewo ali pa mtendere tsopano. Tsono iweyo ndi magulu ako ankhondo ndi mitundu yambiri ya anthu imene ili nawe, mudzabwera ngati mphepo yamkuntho. Mudzaphimba dziko lonse ngati mtambo. “Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Pa tsiku limenelo mumtima mwako mudzaloŵa maganizo ofuna kukonzekera kuchita zoipa. Ndipo udzanena kuti, ‘Ndikukathira nkhondo dziko la midzi yopanda malinga. Ndipita kwa anthu amene amakhala mwamtendere, amene satchinjirizidwa ndi malinga kapena zitseko kapena mipiringidzo. Ndikukaŵalanda chuma chao ndi kufunkha zinthu zao. Ndikukathira nkhondo anthu okhala m'mizinda imene kale inali mabwinja. Ndidzalimbananso ndi anthu amene adasonkhana kuchokera ku maiko ambiri. Anthuwo ali ndi zoŵeta ndi katundu wochuluka, ndiponso amakhala pakatikati pa dziko lapansi.’ Anthu a ku Sheba ndi ku Dedani, ndiponso amalonda a ku Tarisisi ndi midzi yake yonse, adzafunsa kuti, ‘Kodi kutereku, ukudzafunkha? Kodi wasonkhanitsa gulu lako lankhondo kudzanyamula zofunkha, kudzatenga siliva ndi golide, kudzalanda ziŵeto ndi katundu, kuti zikhale zofunkha zochuluka?’ “Nchifukwa chake, iwe mwana wa munthu, ulalike ndipo uuze Gogi kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Pa nthaŵi imene anthu anga Aisraele adzakhale mwamtendere, udzanyamuka. Udzachokera kwanu ku mbali zakutali kumpoto, pamodzi ndi mitundu yambiri ya anthu, onsewo okwera pa akavalo, gulu lankhondo lalikulu ndi lamphamvu. Udzabwera kudzalimbana ndi anthu anga Aisraele, ngati namondwe woononga dziko lapansi. Masiku amenewo iwe Gogi ndidzakuyambanitsa ndi dziko langa kuti anthu a mitundu yonse adzandidziŵe, pamene ndidzaonetse kuyera kwanga pa zimene ndidzakuchite iweyo Gogi. “Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Kodi iwe si ndiwe amene ndidalankhula za iwe masiku amakedzana, kudzera mwa atumiki anga aneneri a ku Israele? Pa zaka zambiri iwo ankalengeza kuti ndidzautsa iwe kuti udzalimbane ndi Aisraele. Pa nthaŵi imeneyo, pamene Gogi adzabwera kudzalimbana ndi dziko la Israele, mkwiyo wanga udzayaka zedi. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. Chifukwa cha mkwiyo ndi ukali wanga woyakawo, ndikulumbira kuti kudzachita chivomezi chachikulu m'dziko lonse la Israele. Nsomba za m'nyanja ndi mbalame zamumlengalenga, nyama zakuthengo ndi zokwaŵa zonse, pamodzi ndi anthu onse okhala pa dziko lapansi, zonsezo zidzanjenjemera ndi mantha. Mapiri adzaphwanyika, magomo adzanyenyeka, ndipo makoma onse adzagwa pansi. Gogi ndidzamuutsira nkhondo kuchokera ku mapiri anga onse. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. Anthu a Gogiyo adzaphana okhaokha ndi malupanga. Ndidzamulanga ndi mliri ndi imfa. Ndidzagwetsa mvula yoopsa ndi matalala ndiponso sulufure ndi miyala yamoto pa iye, pa magulu ake ankhondo ndiponso pa mitundu yonse ya anthu omperekeza. Umu ndimo m'mene ndidzaonetsere kuti ndine wamphamvu ndi woyera. Choncho ndidzadziŵika kwa anthu a mitundu yonse. Tsono adzadziŵadi kuti Ine ndine Chauta.” “Iwe mwana wa munthu, ulalike zodzudzula Gogi. Umuuze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndikudana nawe iwe Gogi, kalonga wamkulu wa ku Meseki ndi ku Tubala. Ndidzakuzunguza ndi kukupirikitsira m'tsogolo. Ndidzakutenga kuchokera ku maiko akutali kumpoto, ndipo ndidzakutuma kuti ukalimbane ndi anthu okhala m'mapiri a ku Israele. Pambuyo pake ndidzathyola uta wa ku dzanja lako lamanzere, ndipo ndidzagwetsa mivi ya ku dzanja lako lamanja. Udzagwa ku mapiri a ku Israeleko, iweyo pamodzi ndi magulu ako onse ankhondo ndi onse amene amakuthandiza. Ndidzakusandutsa chakudya cha miimba ndi cha zilombo zakuthengo. Udzafera kuthengo, poti ndagamula choncho Ineyo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. Ndidzagwetsa moto pa dziko la Magogi ndi pa onse amene amakhala mwamtendere m'mbali mwa nyanja. Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta. Ndidzamveketsa dzina langa loyera pakati pa anthu anga Aisraele. Ndipo sindidzalola kuti dzina langa liipitsidwenso. Anthu a m'maiko onse adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndine Woyera uja wa ku Israele. “Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndithu zilikudza, zidzachitikadi. Ndiye tsiku limene ndidanena lija. Okhala m'mizinda ya Aisraele adzatuluka ndipo adzasonkhanitsa zida zankhondo zosiyidwa kuti azitenthe ngati nkhuni: ndiye kuti zishango ndi lihawo, mauta ndi mivi, zibonga ndi mikondo. Adzazisonkhere moto pa zaka zisanu ndi ziŵiri. Sadzatolera nkhuni ku thengo kapena kusalika zina ku nkhalango. Moto wao azidzasonkha ndi zidazo. Motero adzafunkha oŵafunkha, ndipo adzabera oŵabera. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. “Pa tsiku limenelo Gogi ndidzampatsa malo a manda oti amuikemo ku dziko la Israele, m'chigwa cha anthu apaulendo, kuvuma kwa Nyanja Yakufa. Chigwacho chidzatsekera njira anthu odzera kumeneko, chifukwa Gogi ndi gulu lake lankhondo adzaikidwa kumeneko, ndipo chigwacho chidzatchedwa chigwa cha gulu lankhondo la Gogi. Aisraele adzakhala akukwirira mitembo pa miyezi isanu ndi iŵiri, kuti ayeretse dziko. Anthu onse am'dzikomo adzakwirira nao, ndipo ntchito imeneyo adzatchuka nayo pa tsiku limene ndidzaonetse ulemerero wanga. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. Miyezi isanu ndi iŵiri itapita, adzasankha anthu odzayendera m'dziko lonselo, kuti azifunafuna mitembo imene idatsalira ndi kumaikwirira, motero adzaliyeretseratu dzikolo. Popita m'dzikomo, azidzati wina akaona fupa la munthu, azidzaika chizindikiro pambali pake, mpaka fupalo litakwiriridwa m'chigwa cha gulu lankhondo la Gogi. Komwekonso kudzakhala mzinda wotchedwa Gulu lankhondo. Motero dzikolo lidzakhala loyeretsedwa.” “Ndiye iwe mwana wa munthu, Ine Ambuye Chauta mau anga ndi aŵa: Uitane mbalame ndi nyama zonse zakuthengo, uziwuze kuti, ‘Sonkhanani mubwere kuno. Musonkhane kuchokera kumbali zonse. Mubwere ku phwando limene ndikukukonzerani ku mapiri a Israele. Phwando lake ndi lansembe. Kumeneko mudzadya nyama ndi kumwa magazi. Mudzadya nyama ya ankhondo amphamvu, ndipo mudzamwa magazi a akalonga a dziko lapansi. Onsewo adaphedwa ngati nkhosa zamphongo, anaankhosa, mbuzi ndiponso ngati ng'ombe zamphongo zonenepa za ku Basani. Ku phwando lansembe limene ndikukukonzeranilo, mudzadya zonona mpaka kukhuta, mudzamwa magazi mpaka kuledzera. Zoonadi ku tebulo langa mudzakhuta podya akavalo ndi okwerapo ake, ankhondo amphamvu ndi asilikali amitundumitundu. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. “ ‘Ndidzaonetsa ulemerero wanga pakati pa anthu a mitundu yonse. Ndipo adzaona m'mene ndidzaŵalangire ndi dzanja langa, limene ndidzaŵasanjike. Kuyambira tsiku limenelo mpaka m'tsogolo mwake, Aisraele adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta Mulungu wao. Anthu a m'maiko onse adzadziŵa kuti Aisraele adaatengedwa ukapolo chifukwa cha machimo ao, chifukwa anali osakhulupirika kwa Ine. Choncho ndidaŵafulatira, ndipo ndidaŵapereka m'manja mwa adani ao. Motero onsewo adafa pa nkhondo. Ndidaŵachita zimenezi chifukwa cha kunyansa kwao ndi machimo ao, ndipo ndidaŵafulatiradi. “ ‘Tsono zimene Ine Ambuye Chauta ndikunena ndi izi: Tsopano a m'fuko la Yakobe ndidzaŵakhazikanso pabwino. Aisraelenso onse ndidzaŵachitira chifundo. Dzina langa loyera ndidzaliteteza. Anthuwo akadzakhazikika mwamtendere m'dziko lao, popanda wina woŵavuta, pamenepo adzaiŵala zamanyazi zao zimene zidaŵagwera chifukwa chosandikhulupirira Ine. Ndidzaŵabwezera kwao kuŵachotsa pakati pa mitundu ina ya anthu, ndi kuŵasonkhanitsa kuchokera ku maiko a adani aowo. Motero ndidzaonetsa pamaso pa mitundu yambiri ya anthu kuti ndinedi Woyera. Choncho adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta Mulungu wao. Paja ndidaaŵatumiza ku ukapolo pakati pa mitundu ina ya anthu, kenaka ndidaŵabwezanso onse ku dziko lao, osasiyako ndi mmodzi yemwe. Sindidzaŵafulatiranso, popeza kuti ndidzatumiza mzimu wanga kwa Aisraele. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.’ ” Ku mayambiriro a chaka, tsiku lakhumi la mwezi, chaka cha 25 cha ukapolo wathu, ndiye kuti patapita zaka khumi ndi zinai Yerusalemu ataonongedwa, dzanja la Chauta lidandigwira nkupita nane ku Yerusalemu. Ngati kutulo Chauta adapita nane ku dziko la Israele, nandiika pa phiri lalitali pamene ndidaona ngati mzinda. Atandifikitsa kumeneko, ndidaona munthu wonyezimira ngati mkuŵa. M'manja mwake anali ndi chingwe chabafuta ndi bango loyesera, ndipo adaaimirira pa chipata. Munthuyo adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, penyetsetsa ndipo umvetsetse bwinobwino. Uikepo mtima pa zonse zimene ndikukuwonetsa, pakuti chimenechi ndicho chifukwa chake chimene adakubweretsera kuno. Tsono ukaŵauze Aisraele zonse zimene uziwonezi.” Tsono ndidaona chipupa chozinga Nyumba ya Mulungu ponseponse. Munthu uja anali ndi bango lopimira m'manja mwake. Bangolo kutalika kwake linali mamita atatu. Adapima kuchindikira kwa chipupacho napeza kuti ndi bango lathunthu. Kutalika kwake cham'mwamba kunalinso bango lathunthu. Adapita ku chipata choyang'ana kuvuma, adakwera pa makwerero ake napima chiwundo cha pachipatapo, kutalika kwake kunali bango lathunthu. Panalinso zipinda za alonda, ndipo chilichonse chinali bango lathunthu m'litali mwake, chimodzimodzinso mu ufupi mwake, bango lathunthu. Mipata ya pakati pa zipindazo inali ya mamita aŵiri ndi theka. Ndipo chiwundo cha pachipata pafupi ndi khonde lam'kati lapachipata, chinali bango lathunthu. Adapima khonde lam'kati lapachipata, napeza kuti linali la mamita anai. Mphuthu zake zinali mita limodzi kuchindikira kwake. Khonde lam'kati lapachipata linali kumapeto kwenikweni pafupi ndi Nyumba ya Mulungu. M'kati mwa chipata chakuvumacho munali zipinda za alonda zitatu mbali iliyonse. Zitatu zonsezo zinali zolingana, ndipo mphuthu zake pa mbali zonse zinali zolingananso. Pambuyo pake adapima chipata choloŵera. Chinali cha mamita asanu muufupi mwake. M'litali mwake chinali cha mamita 6 ndi theka. Kumaso kwa zipinda za alonda zija kunali kachipupa ka mita limodzi m'litali mwake ndi muufupi momwe. Zipinda zitatuzo zinali za mamita atatu mbali zonse. Tsono adayesa kutalika kuchokera ku khoma lakumbuyo la chipinda chimodzi mpaka ku khoma la chipinda china, kuchokera ku chitseko mpaka kuchitseko china. Kutalika kwake kunali mamita 12 ndi theka. Pambuyo pake adayesa khonde lam'kati, linali la mamita khumi. Ndipo pozungulira khondelo panali bwalo. Kuchokera pa khomo lapachipata mpaka ku mapeto a khonde la chipata cham'kati, kutalika kwake kunali mamita 25. Makoma a zipinda zija ndiponso makoma a pakati pa zipindazo anali ndi mazenera. Khonde lam'kati linali nawonso mazenera m'kati mwake. Pa makoma onse adaazokotapo zithunzi za kanjedza. Tsono munthu uja adandiloŵetsa m'bwalo lakunja, ndipo ndidaona zipinda ndi mseu wamiyala kuzungulira bwalo lonse. Zipinda zonse pamodzi zinali makumi atatu ndipo zinkayang'ana mseuwo. Mseuwo unkayenda m'mphepete mwa zipata zija, molingana ndi kutalika kwake kwa zipatazo. Umenewu unali mseu wam'munsi. Tsono adayesa m'kati mwa bwalo kuchokera ku chipata cham'munsi mpaka ku chipata chakunja cha bwalo lam'kati. Kutalika kwake kunali mamita makumi asanu. Pambuyo pake munthuyo adayesa chipata chakumpoto chopitira ku bwalo lakunja. Adayesa m'litali mwake ndi muufupi mwake. Zipinda za alonda zimene zinali zitatu pa mbali iliyonse, mphuthu zake ndiponso khonde lake lam'kati, zonse zinali zolingana ndi za chipata choyamba chija. M'litali mwake chinali mamita 25, ndipo muufupi mwake chinali mamita 12 ndi theka. Mazenera ake, khonde lake lam'kati ndiponso kanjedza wozokota uja, zonse zinali zolingana ndi zachipata choyang'ana kuvuma. Chipatacho chinali ndi makwerero asanu ndi aŵiri, ndipo khonde lake linali cham'kati. Chipata chonga chakuvuma chija chidakaloŵa ku bwalo lam'kati moyang'anana ndi chipata chakumpoto. Adachiyesa kuchokera ku chipata china mpaka ku chipata china, kutalika kwake kunali mamita makumi asanu. Pambuyo pake munthu uja adapita nane kumwera, ndipo ndidaona chipata choyang'ana kumwera. Adayesa mphuthu zake ndi khonde lake lam'kati, zinali zolingana ndi zinzake zija. M'zipinda za chipata chimenechi ndi m'khonde lake lam'kati munali mazenera onga a m'zipinda zina. M'litali mwake munali mamita 25, muufupi mwake munali mamita 12 ndi theka. Panalinso makwerero asanu ndi aŵiri, ndipo khonde lake linali cham'kati. Pa mphuthu zake adaazokotapo zithunzi za kanjedza uku ndi uku. Bwalo lam'kati linali ndi khomo loyang'ana kumwera. Adaliyesa kuchokera ku chipata chimenechi mpaka ku chipata chakunja, kutalika kwake kunali mamita makumi asanu. Munthu uja adandiloŵetsa m'bwalo lam'kati kudzera ku chipata chakumwera. Adayesa chipatacho, chinali cholingana ndi zinzake zija. Zipinda zake, mphuthu zake ndi khonde lake lam'kati zinalinso zolingana ndi zinzake zija. Zipindazo zinali ndi mazenera kuzungulira ponse ndiponso m'khonde mwake. M'litali mwake munali mamita 25, muufupi mwake munali mamita 12 ndi theka. Tsono panali makonde pozungulira ponse. Lililonse m'litali mwake munali mamita 12 ndi theka, muufupi mwake mamita aŵiri ndi theka. Khonde lake lam'kati lidaayang'ana bwalo lakunja. Pa mphuthu zake adaazokotapo zithunzi za kanjedza, ndipo linali ndi makwerero asanu ndi atatu. Kenaka munthuyo adapita nane m'bwalo lam'kati chakuvuma. Adachiyesa chipatacho napeza kuti chinali cholingana ndi zinzake zina. Zipinda zake, mphuthu zake ndiponso khonde lake lam'kati zinali zolingana ndi zinzake zija. Zipindazo zinali ndi mazenera kuzungulira ponse, ndiponso m'khonde mwake. M'litali mwake munali mamita 25, muufupi mwake mamita 12 ndi theka. Khonde lake lam'kati lidaayang'ana bwalo lakunja, ndipo pa mphuthu zake adaazokotapo zithunzi za kanjedza uku ndi uku. Linali ndi makwerero asanu ndi atatu. Pambuyo pake adapita nane ku chipata chakumpoto. Adachiyesa napeza kuti ncholingana ndi zinzake zija. Zipinda zake, mphuthu zake ndi khonde lake lam'kati zinali chimodzimodzi. Linali ndi mazenera kuzungulira ponse. M'litali mwake munali mamita 25, muufupi mwake mamita 12 ndi theka. Khonde lake lam'kati lidaayang'ana bwalo lakunja. Pa mphuthu zake adaazokotapo zithunzi za kanjedza uku ndi uku, ndipo linali ndi makwerero asanu ndi atatu. Panali chipinda ndi khomo lake pafupi ndi khonde lam'kati la kuchipata kumene ankatsukirako nyama ya nsembe zopsereza. M'khondemo munali matebulo aŵiri, lina uku lina uku. Ankapherako nyama za nsembe zopsereza, nsembe zopepesera machimo ndiponso nsembe zopepesera kupalamula. Kunja kwake kwa khonde lam'kati lija la ku chipata chakumpoto kunali matebulo aŵiri. Panali matebulo anai cham'kati, ndiponso anai ena chakunja kwa chipatacho. Onse pamodzi anali matebulo asanu ndi atatu. Pamatebulopo ankapherako nyama za nsembe zopsereza. Matebulo anai a nsembe zopsereza anali a miyala yosema. Lililonse m'litali mwake linali la masentimita 75, muufupi mwake linali la masentimita 75, ndipo msinkhu wake unali wa masentimita 50. Patebulopo ankaikapo zipangizo zophera nsembe zopserezazo ndi nsembe zina. Motero nyama ya nsembezo ankaiika pa matebulowo. Ndipo mbedza zitalizitali ngati chikhatho anakazimangirira pozungulira ponse cham'kati. Tsono munthu uja adapita nane m'kati mwenimweni mwa bwalo. Ndidaonamo zipinda ziŵiri m'kati mwa bwalolo. China chinali pafupi ndi chipata chakumpoto kuyang'ana kumwera. China chinali pafupi ndi chipata chakumwera kuyang'ana kumpoto. Tsono adandiwuza kuti, “Chipinda choyang'ana kumwerachi ncha ansembe oyang'anira Nyumba ya Mulungu. Chipinda choyang'ana kumpotochi ncha ansembe oyang'anira za guwa lansembe. Ameneŵa ndiwo ana a Zadoki, ndipo ndi okhawo mwa zidzukulu za Levi amene angafike kufupi kudzatumikira Chauta. “Tsono munthu uja adayesa bwalolo, linali lolingana m'litali ndi muufupi mwake, mamita 50 mbali iliyonse. Ndipo guwa linali kumaso kwa Nyumba ya Mulungu. Pambuyo pake adapita nane m'khonde lam'kati la Nyumba ya Mulunguyo. Adayesa mphuthu za khondelo zinali za mamita aŵiri ndi theka mbali zonse. Muufupi mwake mwa chipata munali mamita asanu ndi aŵiri. Zipupa za pambali pa chipata zinali za mita limodzi ndi theka mbali zonse. Khonde lam'kati m'litali mwake linali la mamita khumi, muufupi mwake mamita asanu ndi limodzi. Panali makwerero khumi, ndipo pambali pa mphuthu panali nsanamira ku mbali zonse.” Pambuyo pake munthu uja adapita nane m'chipinda chopatulika cha Nyumba ya Mulungu, nayesa mphuthu zake. Muufupi mwake munali mamita atatu mbali iliyonse. Muufupi mwake mwa khomo munali mamita asanu. Zipupa zake zam'mbali zinali za mamita aŵiri ndi theka muufupi mwake mbali iliyonse. Adayesa kutalika kwake kwa chipindacho, kunali mamita makumi aŵiri, muufupi mwake mamita khumi. Kenaka adakaloŵa m'kati nakayesa mphuthu zapakhomo. Zinali za mita limodzi, ndipo khomolo linali la mamita atatu. Zipupa za m'mbali mwa khomolo zinali za mamita atatu ndi theka mbali iliyonse. Pambuyo pake adayesa chipinda chenichenicho napeza kuti m'litali mwake ndi muufupi mwake munali mamita khumi. Apo adandiwuza kuti, “Chimenechi ndicho chipinda chopatulika kwambiri.” Tsono munthu uja adayesa khoma la Nyumba ya Mulungu, linali la mamita atatu. Panali zipinda zina kuzungulira Nyumbayo, chilichonse muufupi mwake chinali cha mamita aŵiri. Zipindazo zinali zitatu zosanjikizana, chigawo chilichonse chinali ndi zipinda makumi atatu. Pa makoma a Nyumba ya Mulunguyo panali zochirikiza zipindazo, kuti zisamatsamire pa chipupa cha Nyumba ya Mulungu. Zipinda zam'mbalizo zinkapita zikukulirakulira pomakwera chipinda ndi chipinda, potsata kukulirakulira kwa zochirikiza za zipinda zija. Pambali pa Nyumba ya Mulungu panali makwerero okwerera pamwamba, kuchokera chigawo chapansi kudzera chapakati, mpaka kukafika chapamwamba. Tsono ndidaona chiwundo chozungulira Nyumba ya Mulungu. Chidapanga maziko a zipindazo, ndipo chinali cha mamita atatu. Khoma la kunja kwa zipindazo linali la mamita aŵiri ndi theka kuchindikira kwake. Pakati pa chiwundocho ndi zipinda za Nyumba ya Mulunguyo panali bwalo la mamita khumi m'kupingasa kwake, kuzungulira Nyumba yonseyo. Zipinda zam'mbalizo zinali zotsekulira ku mbali za chiwundo. Chitseko chimodzi chinkayang'ana kumpoto, china chinkayang'ana kumwera. Kukula kwa chiwundo chosamangapo kanthu kunali mamita aŵiri ndi theka kuzungulira ponseponse. Chakuzambwe, kuyang'anana ndi bwalo la Nyumba ya Mulungu, kunali nyumba inanso ya mamita 35 muufupi mwake. Khoma lake linali la mamita aŵiri ndi theka kuchindikira kwake kuzungulira ponseponse, m'litali mwake linali la mamita 45. Tsono munthu uja adayesa Nyumba ya Mulungu, m'litali mwake inali ya mamita makumi asanu. Bwalo la Nyumbayo ndi makoma ake, zonse zinali za mamita makumi asanu. Kumaso kwa Nyumba ya Mulungu chakuvuma kwa bwalolo muufupi mwake munali mamita makumi asanu. Kenaka adayesa kutalika kwa nyumba yoyang'anana ndi bwalolo chakuzambwe kwa Nyumba ya Mulungu, ndi njira zam'kati ku mbali iliyonse. Zonsezo zinali za mamita makumi asanu. Chipinda cha m'thunthu mwa Nyumba ya Mulungu, chipinda cham'kati ndiponso khonde lam'kati loyang'ana kunja, mazenera ndi made ake, zonsezo zinali zochingidwa ndi matabwa. Pamwamba, kupenyana ndi chiwundo, Nyumba ya Mulungu idaakutidwa ndi matabwa kuyambira pansi mpaka ku mazenera, ndipo mazenerawo anali okutidwa. Pamwamba pa khomo loloŵera ku chipinda cham'kati, adaazokotapo zithunzi za akerubi ndi za kanjedza. Kerubi mmodzi adaakhala pakati pa kanjedza muŵiri. Kerubi aliyense anali ndi nkhope ziŵiri: ina inali nkhope ya munthu, yoyang'ana kanjedza wa mbali imodzi, ina inali nkhope ya mkango yoyang'ana kanjedza wa mbali ina. Zidachingidwa choncho kuzungulira Nyumba yonse. Motero kuyambira pansi mpaka pamwamba pa zitseko panali zithunzi zozokota za akerubi ndi za kanjedza. Mphuthu za chipinda cham'thunthu kutalika kwake mbali zonse kunali kolingana. Kumaso kwa malo opatulika kunali chinthu chooneka ngati guwa lansembe la matabwa. Msinkhu wake unali wa mita limodzi ndi hafu, m'litali mwake munali mita limodzi, muufupi mwake munalinso mita limodzi. Mphuthu zake, tsinde lake ndi makoma ake, zonse zinali zopanga ndi mtengo. Munthu uja adandiwuza kuti, “Tebulo limeneli ndilo limene limakhala pamaso pa Chauta.” Chipinda cham'thunthu chija chinali ndi zitseko ziŵiri, malo oyera analinso ndi zitseko ziŵiri. Pa chitseko chilichonse panali zigawo ziŵiri zopatukana. Pazitsekopo adazokotapo zithunzi za akerubi ndi za kanjedza, monga pa makoma aja. Kunja kwake kunali ngati denga lamatabwa pamwamba pa khonde lam'kati. Pa mbali zonse za khonde lam'katilo panali mazenera, ndipo pa zipupa zake zonse adazokotapo zithunzi za kanjedza. Pambuyo pake munthu uja adapita nane ku bwalo lakunja chakumpoto, nandiloŵetsa m'nyumba ina yoyang'anana ndi bwalo la Nyumba ya Mulungu ndi nyumba ina yakumpoto. Nyumba yakumpotoyi m'litali mwake inali ya mamita makumi asanu, muufupi mwake inali ya mamita 25. Kuyang'anana ndi bwalo lam'kati la mamita khumi, ndiponso kuyang'anana ndi chiwundo cha bwalo lakunja, panali makonde atatu osanjikana. Kumaso kwa zipindazo kunali njira yam'kati, muufupi mwake mamita asanu, m'litali mwake mamita makumi asanu. Makomo ake adaaloza kumpoto. Zipinda zam'mwamba zinali zazifupi m'mimbamu kupambana zam'munsi ndi zapakati, chifukwa njira zake zam'kati zidaalanda malo ambiri. Zonse zinali zosanjikana patatu, ndipo zinalibe nsanamira monga za mabwalo. Motero zipinda zam'mwamba zinali zochepera kuyerekeza ndi zapakati ndi zapansi. Khoma lakunja, kutalika kwake mamita 25, linkatsatana ndi zipinda kutsogolo kwake pambali pa bwalo lakunja. Zipinda za m'mbali mwa bwalo lakunja m'litali mwake zinali za mamita 25. Koma zokhala m'mbali mwa Nyumba ya Mulungu ija m'litali mwake zinali za mamita makumi asanu. Pansi pa zipinda zimenezi panali khoma lake chakuvuma, kuchokera ku bwalo lakunja kumene khoma la bwalo linkayambira. Mbali yakumwera, kuyang'anana ndi bwalo ndi nyumbayo, kunali zipinda zina, ndipo kumaso kwake kunali njira. Zipinda zimenezi m'litali mwake ndi muufupi mwake ndiponso maonekedwe ake onse zinali zolingana ndi zoyang'ana kumpoto zija. Makomo ake ndi zitseko zake zinalinso zolingana. Ndipo kunsi kwa zipinda zakumwera, kunali khomo lake mbali ya kuvuma kumene ankaloŵerako. Kunalinso khoma logaŵa zipinda. Tsono munthu uja adandiwuza kuti, “Zipinda zakumpoto ndi zakumwera zoyang'anana ndi khonde nzoyera. M'menemo ansembe okhala kufupi ndi Chauta amadyeramo zopereka zopatulika kwambiri. M'menemo adzaikamo zopereka zimenezi pamodzi ndi zopereka za chakudya, nsembe yopepesera machimo, ndi nsembe zopepesera kupalamula, poti malowo ndi oyera. Ansembe ataloŵa m'malo oyerawo, sadzatulukamo kupita m'bwalo lakunja popanda kusiya m'menemo zovala zimene amavala potumikira zija. Zimenezi nzoyera. Ayenera kuvala zina asanafike pa anthu.” Atamaliza kuyesa m'kati mwa Nyumba ya Mulungu, munthu uja adatuluka nane pa chipata chopenya kuvuma. Pamenepo adayesa bwalo lonse. Adayesa mbali yakuvuma ndi bango loyesera lija, kutalika kwake kunali kwa mamita 250. Kenaka adatembenuka nayesa mbali yakumpoto ndi bango lakelo, kutalika kwake kunali kwa mamita 250. Adatembenuka nayesa mbali yakumwera ndi bango lake. Kutalika kwake kunali kwa mamita 250. Adatembenukanso nayesa kuzambwe ndi bango lake. Kutalika kwake kunali kwa mamita 250. Motero adayesa mbali zonse zinai. Panali khoma lozungulira bwalo lonselo, m'litali mwake linali la mamita 250, muufupi mwakenso mamita 250. Khomalo linali lolekanitsa zinthu zoyera ndi zinthu wamba. Pambuyo pake munthu uja adapita nane ku chipata choyang'ana kuvuma. Kumeneko ndidaona ulemerero wa Mulungu wa Israele ukuchokera kuvuma. Liwu lake linali ngati mkokomo wa madzi, ndipo dziko lapansi lidaŵala ndi ulemerero wakewo. Zimene ndidaziwona m'masomphenya zinali ngati zomwe ndidaaziwona zija pamene Chauta adaabwera kudzaononga mzinda. Zinalinso ngati zimene ndidaaziwona ku mtsinje wa Kebara. Tsono ndidadzigwetsa pansi chafufumimba. Ulemerero wa Chauta udakaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, kuloŵera chipata choyang'ana kuvuma. Mzimu wa Mulungu udandinyamula numandiloŵetsa m'bwalo lam'kati. Ndipo ulemerero wa Chauta udadzaza Nyumba yakeyo. Munthu uja ataima pambali panga, ndidamva wina akundilankhula kuchokera m'Nyumba ya Mulungu. Adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, malo ano ndi malo a mpando wanga waufumu, malo amene ndimapondapo mapazi anga. Kuno ndiye kumene ndidzakhale pakati pa anthu anga Aisraele mpaka muyaya. Iwowo ngakhalenso mafumu ao, sadzaipitsanso dzina langa loyera pokhala osakhulupirika kapena poika mitembo ya mafumu ao ku zitunda zachipembedzo. Ankamanga chiwundo chao pafupi ndi changa ndiponso mphuthu zao pafupi ndi zanga, nkungokhala khoma chabe pakati pa iwowo ndi Ine. Motero ankaipitsa dzina langa loyera ndi zonyansa zao zimene ankachita. Tsono ndidaŵaononga ndili wokwiya. Tsopano aleke zonyansa zao, aleke kupembedza milungu ina, ndipo achotse mitembo ya mafumu ao, isakhalenso pafupi ndi Ine. Apo Ine ndidzakhala pakati pao mpaka muyaya. “Iwe mwana wa munthu, uŵauze Aisraele za Nyumba ya Mulunguyi, maonekedwe ake ndi mamangidwe ake, kuti achite manyazi ndi machimo ao. Akachita manyazi ndi zoipa zonse zimene adachita, uŵasimbire za Nyumba ya Mulungu ndi maonekedwe ake, za makomo ake otulukira ndi oloŵera, za kaonekedwe kake konse ndi za makonzedwe ake onse. Uŵafotokozere malamulo ndi malangizo ake, ndipo uŵalembe iwo akuwona, kuti aziŵakumbukira ndi kumaŵatsatadi. Limeneli ndilo lamulo la Nyumba ya Mulungu imene idzamangidwa pamwamba pa phiri. Pozungulira pake ponse padzakhala poyera kwambiri. Limeneli ndilo lamulo la Nyumba ya Mulungu. “Nayi miyeso ya guwa lansembe potsata miyeso yomwe ija imene adaayesera Nyumba ya Mulungu. Patsinde pake padzakhala ngalande ya masentimita makumi asanu kuzama kwake, ndiponso muufupi mwake. M'milomo mwake mwa ngalandeyo mudzakhala mwa mjintchi wa masentimita 25. Guwalo msinkhu wake udzakhala wotere: kuchokera pa tsinde pansi mpaka pa phaka lapansi mita limodzi, muufupi mwake theka la mita. Kuchokera ku phaka laling'ono mpaka ku phaka lalikulu, msinkhu wake udzakhala mamita aŵiri, muufupi mwake mudzakhala masentimita makumi asanu. Malo osonkhapo moto pa guwa msinkhu wake udzakhala mamita aŵiri. Pamwamba pake padzatuluka nyanga zinai, kutalika kwake theka la mita. Malo osonkhapo motowo kutalika kwake kudzakhala mamita asanu ndi limodzi, muufupi mwakenso mamita asanu ndi limodzi, motero adzakhala olingana mbali zonse. Phaka lapakati lidzakhala la mamita asanu ndi aŵiri kutalika kwake, ndiponso asanu ndi aŵiri muufupi mwake, pa mbali zake zonse zinai. Ndipo mkombero wake udzakhala wa masentimita 25 mjintchi wake. Ngalande ya patsinde pa guwalo idzakhala ya masentimita makumi asanu, ndipo makwerero a paguwapo adzayang'ana kuvuma.” Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, ndikukuuza kuti guwa litamangidwa, malamulo ake popereka nsembe yopsereza ndiponso powaza magazi paguwapo, ndi aŵa: Ansembe a fuko la Levi, am'banja la Zadoki, ndiwo azibwera pafupi nane kudzanditumikira. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. Udzaŵapatse mwanawang'ombe wamphongo kuti aperekere nsembe yopepesera machimo. Utaipha, udzatengeko magazi, ndi kuŵapaka pa nyanga zinai za guwa pa ngodya zinai za phaka, ndiponso kuzungulira mkombero. Motero udzaliyeretsa guwalo ndi kulidalitsa. Kenaka udzatenge ng'ombe yamphongo imene yaperekedwa ngati nsembe yopepesera machimo. Udzaitenthe pa malo ake enieni, m'bwalo la Nyumba ya Mulungu, kunja kwa malo opatulika. M'maŵa mwake udzapereke tonde wopanda chilema, kuti nayenso akhale nsembe yopepesera machimo. Ndi tondeyo udzayeretse guwalo monga momwe udachitira ndi ng'ombe yamphongo ija. Utaliyeretsa kwathunthu guwalo, udzapereke ng'ombe yamphongo yopanda chilema ndi nkhosa yamphongo yopanda chilema. Udzazipereke pamaso pa Chauta, ndipo ansembe adzazithire mchere ndi kuzipereka kuti zikhale nsembe zopsereza kwa Chauta. Tsiku lililonse pa masiku asanu ndi aŵiri uzidzapereka tonde, ng'ombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo, kuperekera nsembe yopepesera machimo. Zonsezo zidzakhale zopanda chilema. Masiku asanu ndi aŵiriwo adzachite mwambo wopepesera milandu ndi kuyeretsa guwa, kuti alipatulire Chauta. Masiku amenewo atatha, kuyambira tsiku lachisanu ndi chitatu mpaka m'tsogolo mwake, ansembe azidzapereka pa guwalo nsembe zanu zopsereza ndiponso nsembe zanu zachiyanjano. Apo ndidzakulandirani. Ndatero Ine Ambuye Chauta.” Munthu uja adapita nane ku chipata cha kunja kwa malo opatulika choyang'ana kuvuma. Chinali chotseka. Tsono adandiwuza kuti, “Chipata ichi chikhale chotseka, osachitsekula. Wina asaloŵerepo ai, poti Ambuye, Mulungu wa Israele, waloŵerapo. Nchifukwa chake chizikhala chotseka. Kalonga yekha angathe kukhala pamenepo ndi kumadya chakudya pamaso pa Chauta. Adzaloŵa ndi kutuluka kudzera m'khonde lam'kati la chipata chimenecho.” Pambuyo pake munthuyo adandidzeretsa pa chipata chakumpoto ndipo tidafika kumaso kwa Nyumba ya Mulungu. Kumeneko ndidaona ulemerero wa Chauta utadzaza Nyumba yakeyo. Pamenepo ndidadzigwetsa chafufumimba. Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, samala bwino, uyang'anitsitse ndipo umvetse bwino zonse zimene ndikuuze za malamulo ndi malangizo okhudza za Nyumba yangayi. Uzindikire bwino amene angaloledwe kuloŵa m'Nyumba ino ndiponso amene sayenera kuloŵamo. Anthu a mtundu waupandu wa Israele uŵauze mau anga akuti, Aisraele inu, lekani zonyansa zanu zonse. Mudaloŵetsa m'malo anga opatulika alendo osaumbalidwa mu mtima ndi m'thupi momwe. Anthuwo adaipitsa Nyumba yanga pamene inu munkandipatsa chakudya, mafuta ndi magazi omwe. Pochita zoipa zoterezi mudaphwanya chipangano changa. M'malo moti muzisamala ndinu zinthu zanga zopatulika, mwasankha alendoŵa kuti aziyang'anira malo anga opatulika. “Tsono zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Mwa alendo amene ali osaumbalidwa mu mtima ndi m'thupi, pasapezeke ndi mmodzi yemwe woloŵa m'malo anga opatulika, ngakhalenso alendo amene amakhala pakati pa Aisraele. “Tsono Alevi amene adaandisiya kutali pa nthaŵi imene Aisraele adaasokera potsata mafano, adzalangidwa chifukwa cha kulakwa kwao. Adzangokhala atumiki chabe ku malo anga opatulika. Adzayang'anira zipata za Nyumba ya Mulungu ndi kugwira ntchito zina zake kumeneko. Adzapha nyama za nsembe zopsereza, ndi za nsembe zina za anthu. Motero adzidzaimirira anthuwo ndi kumaŵatumikira. Iwowo ankatumikira anthu popembedza mafano, ndipo adasokeretsa Aisraele potero. Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikulumbira ndithu kuti ameneŵa ayenera kulangidwa chifukwa cha zolakwa zao. Saloledwa kudzafika pafupi ndi Ine, kuti anditumikire ngati ansembe. Sadzayandikira zinthu zanga zopatulika ndi zopereka zoyera kwambiri. Adzachititsidwa manyazi chifukwa cha ntchito zao zonyansa. Komabe ndidzaŵaika kuti aziyang'anira Nyumba yanga ndi kutumikira pa ntchito zonse zoyenera kuchitika kumeneko. “Koma ansembe a fuko la Levi a m'banja la Zadoki, amene adakhalabe okhulupirika pa ntchito zosamala malo anga opatulika nthaŵi imene Aisraele adaasokera ndi kundisiya Ine, okhawo adzasendera kwa Ine kuti anditumikire. Adzabwera kwa Ine kudzapereka nsembe za mafuta ndi magazi. Ndatero Ine Ambuye Chauta. Iwo okhawo ndiwo adzaloŵe ku malo anga opatulika ndi kudzayandikira tebulo langa kuti anditumikire. Ndiwo amene adzasamalire zinthu zanga. Pamene aloŵa ku chipata cham'kati, azivala bafuta. Asavale chovala chilichonse cha ubweya wankhosa ponditumikira pa zipata za bwalo lam'kati ndiponso m'kati mwa Nyumba yanga. Azivala nduŵira zabafuta kumutu, ndi akabudula abafuta. Asavale chilichonse choŵachititsa thukuta. Potulukira ku anthu a ku bwalo lakunja, azivula zovala zimene anavala potumikira m'kati, ndi kuzisiya m'zipinda zopatulika. Ndipo avale zovala zina, kuwopa kuti angapatsireko kuyera anthu enawo ndi zovala zaozo. “Ansembewo asamete mpala kapena kuŵeta tsitsi lalitali kwambiri, koma azingoliyepula. Wansembe asamwe vinyo pamene ali pafupi kuloŵa m'bwalo lam'kati. Asakwatire mkazi wamasiye wamba kapena mkazi wosudzulidwa. Azikwatira namwali wosadziŵa mwamuna, ŵa fuko la Israele, kapena mkazi wamasiye wa wansembe mnzake. “Ansembe aziphunzitsa anthu anga kusiyanitsa pakati pa zinthu zoyera ndi zinthu wamba, ndiponso pakati pa zinthu zoyenera ndi zosayenera kuperekera nsembe. Pakakhala milandu, ansembe adzakhala oweruza, ndipo adzayenera kugamula milanduyo potsata malamulo anga. Atsate malamulo anga ndi malangizo anga pa za masiku anga onse achikondwerero. Adzasamalenso kuti masiku anga a Sabata akhale oyera. “Wansembe asadziipitse pokhudza munthu wakufa, kupatula ngati ndi bambo wake kapena mai wake, mwana wake wamwamuna kapena wamkazi, mbale wake kapena mlongo wake wosakwatiwa. Ngati aipitsidwa kenaka nkuyeretsedwa, adikire masiku asanu ndi aŵiri, kuti akhale woyeretsedwa kotheratu. Tsono pa tsiku loti aloŵe m'bwalo lam'kati kuti akatumikire m'malo opatulika, apereke nsembe yopepesera machimo. Ndatero Ine Ambuye Chauta. “Ansembe asadzakhale ndi choloŵa chilichonse ai. Choloŵa chao ndine. Ndipo musadzaŵapatse chuma mu Israele. Chuma chao ndine. Iwo azidzadyako za chopereka cha zakudya, za nsembe zopepesera machimo, ndi za nsembe zopepesera kupalamula. Ndipo zonse zoperekedwa kwa Mulungu mu Israele zidzakhala zao. Zopambana pa zonse zoyambirira kucha ndi pa zopereka zina zonse, zidzakhale za ansembe. Muzidzaŵapatsa ufa wanu umene mwayambirira kusinja, kuti choncho m'nyumba mwanu mukhale madalitso. Kaya ndi mbalame kaya ndi nyama, ansembe asadye yofa yokha kapena yochita kujiwa. “Pomadzagaŵa dziko kuti fuko lililonse lilandire chigawo chake, chimodzi adzachipatule kuti chidzakhale cha Chauta. M'litali mwake mudzakhale makilomita 12 ndi theka, muufupi mwake khumi. Malo onsewo adzakhala opatulika. M'kati mwa chigawo chimenechi, malo a mamita 250 mbali iliyonse adzakhala malo a Nyumba ya Mulungu. Pozungulira pake ponse padzakhala malo a mamita 25. M'chigawo chopatulikacho uyese malo a makilomita 12 ndi theka m'litali mwake, makilomita asanu muufupi mwake. Pamenepo padzakhala malo opatulika, malo oyera kwambiri. Malo ameneŵa adzakhalanso a ansembe amene amatumikira ku malo opatulika, amene amayandikira Chauta pomutumikira. Pamenepo padzakhala malo omangapo nyumba zao ndi Nyumba ya Mulungu yomwe. Alevi otumikira ku Nyumba ya Mulungu adzakhala ndi chigawo china cha makilomita 12 ndi theka m'litali mwake, ndi makilomita asanu muufupi mwake. Kumeneko ndiko kudzakhalenso midzi yao. “Poyandikana ndi malo opatulikawo, musankhe kadziko kokwanira makilomita aŵiri ndi theka muufupi mwake, m'litali mwake makilomita 12 ndi hafu, kuti akhale malo a mzinda. Malo ameneŵa adzakhala a banja lonse la Israele. “Mupatulenso dera la mfumu. Likhudzane ndi chigawo cha malo opatulika ndi cha mzinda, liyandikane ndi zigawozo chakuzambwe ndi chakuvuma. Litalike ngati chigawo chimodzi cha fuko la Israele, mpaka kukafika ku malire a dziko kuzambwe ndi kuvuma. Deralo lidzakhala choloŵa cha mfumu m'dziko la Israele. Choncho mafumu anga sadzazunzanso anthu anga, koma azidzaŵalola Aisraele kuti akhale ndi zigawo zaozao. “Mau a Ine Ambuye Chauta ndi aŵa: Tsono pakwana, inu olamulira a ku Israele. Lekani nkhanza ndi kuzunza anthu. Muzimvera malamulo ndipo muzichita zachilungamo. Alekeni anthu anga, musamaŵachotsa pa dziko lao. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. “Miyeso yanu yoyesera zinthu monga efa ndi bati, izikhala yokhulupirika. Efa ndi bati ikhale miyeso yolingana kukula kwake. Muyeso wa homeri ukhale wokwanira mabati khumi, ukhalenso wokwanira maefa khumi. Ndiye kuti kukula kwa miyeso iŵiriyo kuzidzatsata kukula kwa homeriyo. Muyeso wa sekeli ukhale wokwanira magera makumi aŵiri. Muyeso wa mina ukhale wolemera masekeli makumi asanu ndi limodzi. “Nazi zopereka zimene mudzazipereke: chimodzi mwa zigawo 60 za tirigu, barelenso chimodzimodzi, ndiponso chimodzi mwa zigawo 100 za mafuta. Miyeso yake ili motere: mabati khumi alingana ndi homeri imodzi kapena kori imodzi. Mupereke nkhosa imodzi pa gulu la nkhosa 200 za m'mabusa abwino a Israele. Ndimo m'mene mudzaperekere nsembe zatirigu, nsembe zopsereza ndiponso nsembe zachiyanjano, kupepesera milandu ya anthu. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. “Anthu onse a m'dzikomo azipereka zimenezi kwa mfumu ya ku Israele. Ndipo mfumu izipereka zofunikira ku nsembe zopsereza, nsembe zatirigu ndi nsembe zazakumwa pa masiku achikondwerero, ndi a pokhala mwezi, masiku a Sabata, ndiponso pa masiku ena amene Aisraele amaŵasunga. Mfumuyo ipereke zofunikira ku nsembe zopepesera machimo, nsembe zatirigu, nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, kuti zonsezo zikhale zopepesera machimo a Aisraele. “Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, muzitenga mwanawang'ombe wamphongo wopanda chilema, ndi kuchita mwambo woyeretsa malo opatulika. Wansembe atengeko magazi a nsembe yopepesera machimoyo, ndipo aŵapake pa mphuthu za Nyumba ya Mulungu, pa ngodya zinai za pamwamba pa guwa ndi pa mphuthu za pa chipata cha bwalo lam'kati. Muzichita chimodzimodzi pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri la mwezi, kuti mupepesere aliyense amene adachimwa mosafuna kapena mosadziŵa. Motero Nyumba ya Mulungu mudzaisunga yoyera. “Pa tsiku la khumi ndi chinai la mwezi woyamba, muzichita chikondwerero cha Paska, chikondwerero chake cha masiku asanu ndi aŵiri. Masiku amenewo muzidya buledi wosatupitsa. Pa tsiku loyamba la chikondwererocho, mfumu ipereke nsembe ya ng'ombe yamphongo kupepesera machimo ake ndiponso a anthu onse. Pa masiku asanu ndi aŵiri a chikondwererocho, mfumuyo izipereka kwa Chauta nsembe izi zopsereza: ng'ombe zamphongo zisanu ndi ziŵiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziŵiri, zonsezo zopanda chilema. Tsiku lililonse iziperekanso nsembe ya tonde mmodzi, kupepesera machimo. Pamodzi ndi ng'ombe iliyonse yamphongo ndi nkhosa iliyonse yamphongo, mfumu ipereke chopereka cha zakudya chokwanira efa imodzi ndiponso ya mafuta okwanira hini imodzi. “Tsono mfumu ichitenso chimodzimodzi pa tsiku la khumi ndi chisanu la mwezi wachisanu ndi chiŵiri. Chikondwerero chimenecho chizichitika masiku asanu ndi aŵiri. Izipereka nsembe za mtundu womwewonso, zopepesera machimo, nsembe zopsereza, ndiponso nsembe zaufa ndi zamafuta zomwe.” Zimene Ambuye Chauta akunena ndi izi, akuti, “Chipata chakuvuma cha bwalo lam'kati chizikhala chotseka masiku asanu ndi limodzi ogwira ntchito. Azitsekula pa tsiku la Sabata lokha ndi tsiku limene mwezi wakhala. Mfumu poloŵa izidzera m'khonde lam'kati la chipata kuchokera kunja, nkudzaima pafupi ndi nsanamira yapakhomo. Ansembe apereke nsembe yake yopsereza ndi nsembe yachiyanjano. Mfumuyo ipembedze pachiwundopo, kenaka nkutuluka. Koma chipatacho asachitseke mpaka madzulo. Anthu nawonso azipembedza pamaso pa Chauta pa khomo la chipata chimenecho pa masiku a Sabata ndiponso pa tsiku limene mwezi wakhala. Nsembe yopsereza imene mfumu iyenera kupereka kwa Chauta ikhale motere: pa tsiku la Sabata azipereka anaankhosa asanu ndi mmodzi opanda chilema ndiponso nkhosa yamphongo yopanda chilema. Pamodzi ndi nkhosa yamphongo iliyonse, mfumu izipereka ufa wokwanira efa imodzi. Pamodzi ndi anaankhosa aja mfumu iziperekanso ufa monga ingathere. Iperekenso hini imodzi ya mafuta pa efa iliyonse ya ufa. Pa tsiku limene mwezi wakhala mfumu ipereke mwanawang'ombe wamphongo wopanda chilema, anaankhosa asanu ndi mmodzi, ndi nkhosa yamphongo, zonsezo zopanda chilema. Ipereke efa imodzi ya ufa pa ng'ombe yamphongo iliyonse, ndiponso efa ina pa nkhosa yamphongo iliyonse. Pa anaankhosa iperekenso ufa monga m'mene ingathere. Pamodzi ndi efa iliyonse ya ufa, ipereke hini imodzi ya mafuta. Mfumu poloŵa, izidzera m'khonde lam'kati la chipata chakuvuma, nkutulukiranso pomwepo. “Pa masiku achikondwerero, anthu am'dzikomo akabwera kudzapembedza Chauta, munthu woloŵera pa chipata chakumpoto azidzatulukira pa chipata chakumwera. Munthu woloŵera pa chipata chakumwera, azidzatulukira pa chipata chakumpoto. Munthu aliyense asadzatulukire pomwe waloŵera, koma azipita chakutsogolo. Tsono mfumu izidzakhala pakati pao. Izidzaloŵa nthaŵi imene iwowo akuloŵa, nkutuluka nthaŵi imene iwowo akutuluka. “Pa masiku achikondwerero ndi pa masiku ena osankhidwa, zopereka za ufa zikhale zokwanira efa imodzi pamodzi ndi ng'ombe yamphongo iliyonse, efa imodzinso pamodzi ndi nkhosa yamphongo iliyonse, koma pa mwanawankhosa azipereka monga m'mene angathere. Iperekenso hini imodzi ya mafuta pamodzi ndi efa iliyonse ya ufa. Pamene mfumu ikufuna kupereka zaufulu kwa Chauta, monga nsembe yopsereza kapena nsembe zachiyanjano, aitsekulire chipata chakuvuma. Ipereke nsembe yake yopsereza ndi nsembe yake yachiyanjano, monga m'mene imachitira pa tsiku la Sabata. Itamaliza, ituluke. Itatuluka, chipata chitsekedwe. “Tsiku lililonse, nthaŵi yam'maŵa, azipereka kwa Chauta mwanawankhosa wa chaka chimodzi wopanda chilema. Pamodzi ndi nyamayo aziperekanso m'maŵa mulimonse ufa wokwanira chimodzi mwa zigawo zisanu ndi chimodzi za efa. Aziperekanso chimodzi mwa zigawo zitatu za hini ya mafuta okandira ufa wosalala. Nsembe imeneyi yopereka kwa Chautayi iziperekedwa nthaŵi zonse. Motero azipereka mwanawankhosa, ufa ndi mafuta m'maŵa mulimonse, kuti zikhale zopsereza tsiku ndi tsiku.” Zimene Ambuye Chauta akunena ndi izi, akuti, “Kalonga akapereka chigawo cha chuma chake kwa mmodzi mwa ana ake, mphatsoyo ndi ya ana akewodi, popeza kuti ndi chigawo cha choloŵa cha makolo. Koma akapereka mphatso yotere kwa mmodzi mwa atumiki ake, idzakhala ya mtumikiyo mpaka pa chaka cha ufulu. Pamenepo mphatsoyo idzabwerera kwa kalonga uja, chifukwa chuma chake chonse ncha ana okha. Tsono kalonga asalande anthu gawo la chuma chaochao pakuŵachotsa m'dera lao la dziko. Ana ake kalonga aŵapatse choloŵa chao pa dziko limene lili lakelake, kuti choncho asalande ndi mmodzi yemwe mwa ana anga choloŵa chake.” Pambuyo pake munthu uja adandidzeretsa pa khomo la pambali pa chipata nandiloŵetsa ku zipinda zopatulika za ansembe zoyang'ana kumpoto. Ndipo adandilozera malo chakuzambwe kwa zipindazo, nandiwuza kuti, “Aŵa ndi malo m'mene ansembe azidzaphikiramo nyama za nsembe zopepesera kupalamula ndiponso nsembe zopepesera machimo. Kumenekonso ndiko kumene azidzaotcherako chopereka cha chakudya. Sadzatuluka nazo zoyerazi m'bwalo lakunja kuwopa kuti angapatsireko kuyera anthu enawo.” Atatero adandiloŵetsa m'bwalo lakunja napita nane ku ngodya zinai za bwalolo. Tsono m'kati mwa ngodya iliyonse munali bwalo lina. Motero pa ngodya zinai za bwalo lalikululo panali mabwalo ena ang'onoang'ono. Mabwalo amenewo anali ofanana, m'litali mwake mamita makumi aŵiri, muufupi mwake mamita khumi ndi asanu. Kuzungulira mabwalo anai ang'onoang'onowo panali mpanda wamiyala, ndiponso malo osonkhapo moto, omangidwa m'munsi mwa mpandawo. Tsono adandiwuza kuti, “Zimenezi ndizo zipinda zophikiramo, kumene anthu otumikira m'Nyumba ya Mulungu aziphikiramo nyama za nsembe za anthu.” Tsono munthu uja adabwerera nane ku chipata cha ku Nyumba ya Mulungu. Ndidaona kasupe akutuluka kunsi kwa chiwundo choloŵera ku Nyumba ya Mulungu chakuvuma, poti Nyumbayo inali yoyang'ana kuvuma. Kunkayenda madzi kunsi kwa chipupa chakumwera cha Nyumba ya Mulungu, chakumwera kwa guwa. Adanditulutsira pa chipata chakumpoto, nazungulira nane panja pake mpaka ku chipata chakunja choyang'ana kuvuma. Ndipo ndidaona madzi akutuluka chakumwera kwa chipata. Munthuyo adapita chakuvuma ali ndi choyesera m'manja mwake, nayesa mamita mazana asanu. Kenaka adandiwuza kuti ndiloŵe m'madzimo. Madziwo adandilekeza m'kakolo. Adayesanso mamita mazana asanu, nandiloŵetsanso m'madzi muja, ndipo madziwo adandilekeza m'chiwuno. Adayesanso mamita mazana asanu, ndipo madzi adasanduka mtsinje ndithu, ine osatha kuwoloka, poti madziwo adaakwera, anali ozama kwambiri olira kusambira poŵaoloka. Apo adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, waziwonatu zimenezi ati?” Atatero adandibwezera ku gombe la mtsinjewo. Titafika kugombeko, ndidaona mitengo yambiri pa mbali iliyonse ya gombelo. Tsono munthuyo adandiwuza kuti, “Madzi ameneŵa akupita ku chigawo chakuvuma cha dziko kutsikira ku chigwa cha Araba. Potsiriza pake, akakathira m'Nyanja Yakufa imene madzi ake ali oipa, madziwo adzakoma. Kumene mtsinjewo ukuyenda, cholengedwa chilichonse chidzakhala ndi moyo, nsombanso zidzachuluka. Pakuti madzi ameneŵa amapita kumeneko kuti akometse madzi anzake. Ndipo kulikonse kumene mtsinjewo ukuyenda, zonse zidzakhala ndi moyo. Asodzi a nsomba adzakhala pa madooko ao, chifukwa kuyambira ku Engedi mpaka ku Enegilaimu kudzakhala malo abwino oponyako akombe. Mumtsinjewo mudzakhala nsomba zamitundumitundu, monga za m'Nyanja Yaikulu. Koma mataŵale ake ndi maiŵe ake sadzakhala ndi madzi abwino, adzakhalabe amchere. Pambali pa mtsinjewo, pa gombe lililonse, padzakhala mitengo yobereka zipatso za mtundu uliwonse. Masamba ake sadzafota, ndipo zipatso zake zidzakhala zosalekeza. Izidzabereka mwezi uliwonse, chifukwa madzi ake ndi ochokera ku Nyumba ya Mulungu. Zipatso zake anthu azidzadya, ndipo masamba ake azidzachita mankhwala.” Zimene Ambuye Chauta akunena ndi izi, akuti, “Naŵa malire amene mudzatsate poŵagaŵira dziko la Israele mafuko khumi ndi aŵiri aja: Yosefe alandire zigawo ziŵiri. Dzikoli mudzagaŵana mofanana, chifukwa ndidalumbira kuti ndidzalipereka kwa makolo anu ndipo lidzakhala lanulanu. Motero lidzapatsidwa kwa inu mwamaere, kuti likhale choloŵa chanu. Malire ake adzayende motere: chakumpoto kwake achokere ku Nyanja Yaikulu, kutsata mseu wa ku Hetiloni mpaka ku chipata cha Hamati, kupitirira ku Zedati, Berata ndi Sibraimu, mizinda imene ili pakati pa malire a Damasiko ndi Hamati, mpaka ku Hazere-Hatikoni pafupi ndi malire a Haurani. Motero malire akumpoto adzachokera ku nyanja mpaka ku mzinda wa Hazarenoni umene wachitana malire ndi Damasiko chakumpoto, ndiponso mpaka m'malire a Hamati chakumpoto. Imeneyi ndiyo idzakhala mbali yakumpoto.” “Malire akuvuma ayende chakumwera kuchokera ku Hazarenoni pakati pa Haurani ndi Damasiko, kutsata mtsinje wa Yordani pakati pa Giliyadi ndi dziko la Israele, kuloza ku nyanja yakuvuma mpaka ku Tamara. Imeneyi idzakhala mbali yakuvuma.” “Malire akumwera ayende kuchokera ku Tamara mpaka ku dziŵe la Meriboti-Kadesi. Kuchokera kumeneko atsate malire a ku Ejipito mpaka ku Nyanja Yaikulu. Imeneyi ndiyo mbali yakumwera.” “Malire akuzambwe akhale Nyanja Yaikulu mpaka ku malo oyang'anana ndi chipata cha Hamati. Imeneyi ndiyo mbali yakuzambwe.” “Motero mugaŵane dziko limeneli pakati panu potsata mafuko a Israele. Muligaŵe kuti likhale choloŵa chanu. Likhalenso la alendo amene amakhala pakati panu, nabereka ana pakati panu. Alendowo adzakhala nanu ngati mbadwa za mu Israele. Adzapatsidwa choloŵa chao pamodzi ndi inuyo. Mlendo aliyense umpatse choloŵa chake ku fuko limene akukhalakolo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.” “Naŵa maina a mafuko: kuyambira ku malire akumpoto kuchokera ku nyanja, kudzera ku Hetiloni mpaka ku chipata cha Hamati, kukafika ku Hazarenoni, mzinda umene uli kumpoto kwa malire a Damasiko oyang'anana ndi Hamati, ndipo kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, nchigawo chimodzi, ndipo ncha Dani. Kuchitana malire ndi Dani, kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo cha Asere. Kuchitana malire ndi Asere kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo cha Nafutali. Kuchitana malire ndi Nafutali kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo cha Manase. Kuchitana malire ndi Manase kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo cha Efuremu. Kuchitana malire ndi Efuremu kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo cha Rubeni. Kuchitana malire ndi Rubeni kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo cha Yuda. Kuchitana malire ndi Yuda kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo chapadera ndithu. Muufupi mwake chikhale makilomita 12 ndi theka. M'litali mwake chikhale ngati zigawo zina, kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe. Ndipo malo a Nyumba ya Chauta akhale pakati pake.” “Chigawo chimene muchipatule kuti chikhale cha Chauta chikhale cha makilomita 12 ndi theka m'litali mwake, muufupi mwake chikhale cha makilomita khumi. Chigawocho chigaŵidwe motere: chigawo cha Ansembe chikhale cha makilomita 12 ndi theka kumpoto. Kuzambwe chikhale cha makilomita khumi. Kuvuma chikhale cha makilomita asanu. Kumwera chikhale cha makilomita 12 ndi theka. Malo a Nyumba ya Chauta akhale pakatimpakati. Chimenechi chikhale chigawo cha ansembe opatulika, ana a Zadoki, amene adamvera malamulo anga, osatsata Aisraele pamene adaasokera, monga m'mene adaachitira Alevi. Chigawo chimenechi, pakati pa zigawo zonse, chidzakhale mphatso yapadera kwa ansembewo, ndipo chikhale chopatulika kwambiri. Chichitane malire ndi dziko la Alevi.” “Tsono chigawo cha Alevi chikhale choyandikana ndi chigawo cha ansembe. M'litali mwake chikhale cha makilomita 12 ndi theka. Muufupi mwake chikhale cha makilomita asanu. Chigawo chonsechi m'litali mwake mukhale cha makilomita 12 ndi theka, ndipo muufupi mwake mukhale makilomita asanu. Asagulitse kapena kusinthitsa mbali iliyonse ya chigawo chimenechi. Ndi chigawo chapadera ndithu ndipo asachipatse ena, pakuti ndi malo opatulikira Chauta.” “Chigawo chotsala muufupi mwake chikhale cha makilomita aŵiri ndi hafu, m'litali mwake makilomita 12 ndi theka. Chikhale malo omangapo mzinda ndiponso busa. Mzinda ukhale pakatimpakati. Miyeso yake ikhale iyi: Kumpoto kutalika kwake kukhale mamita 2,250. Kumwera kutalika kwake kukhale mamita 2,250. Kuvuma kutalika kwake kukhale mamita 2,250. Kuzambwe kutalika kwake kukhale mamita 2,250. Dera la busa likhale motere: kumpoto kutalika kwake kukhale mamita 125. Kumwera kutalika kwake kukhale mamita 125. Kuvuma kutalika kwake kukhale mamita 125. Ndipo kuzambwe kutalika kwake kukhale mamita 125. Chigawo chotsala pafupi ndi chigawo chopatulika, kutalika kwake makilomita asanu kuvuma, makilomita asanu kuzambwe. Chikhale dziko la minda ya anthu ogwira ntchito mu mzinda. Anthu ogwira ntchito mu mzinda, ochokera m'fuko lililonse la Israele, ndipo azilima chigawocho. Tsono chigawo chathunthu chopatulikacho chikhale cha makilomita 12 ndi theka mbali zonse, ndiye kuti chigawo chopatulikacho pamodzi ndi kadziko ka mzindawo.” “Tsono chigawo chotsala pa mbali zonse ziŵiri za chigawo chopatulika ndi za kadziko ka mzinda, chikhale cha mfumu. Chidzayenda motere: kuyambira m'malire a chigawo chopatulika kukalekeza m'malire akuvuma, mbali ina kuyambiranso m'malire a chigawo chopatulika kukalekeza m'malire akuzambwe, kumapaza kufupi ndi zigawo za mafuko, dera lonselo likhale la mfumu. Chigawo chopatulika ndi malo oyera a Nyumba ya Mulungu zikhale pakatimpakati. Chigawo cha Alevi ndi chigawo cha mzinda zikhale pakati pa dera la mfumulo. Dera limenelo lidzakhale pakatimpakati pa dziko la Yuda ndi la Benjamini.” “Za mafuko ena otsala zidzayenda motere: kuyambira kuvuma mpaka kuzambwe padzakhala chigawo chimodzi, chimenechi ncha Benjamini. Kuchitana malire ndi Benjamini, kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo cha Simeoni. Kuchitana malire ndi Simeoni, kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo cha Isakara. Kuchitana malire ndi Isakara, kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo cha Zebuloni. Kuchitana malire ndi Zebuloni, kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo cha Gadi. Malire a Gadi mbali yakumwera ku Negebu achokere kumwera kuyambira ku Tamara mpaka ku Dziŵe la Meriboti-Kadesi, kenaka kuchokera ku Mtsinje wa ku Ejipito, kukafika ku Nyanja Yaikulu. Dziko lonselo ndilo mupatse mafuko a Israele kuti likhale choloŵa chao. Zigawo zimenezi zidzakhala zao. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.” “Aŵa ndiwo akhale makomo otulukira mu mzinda, ndipo atchulidwe maina a mafuko a Aisraele. Kumpoto, kumene kutalika kwake ndi kwa mamita 2,250, kukhale zipata zitatu: chipata cha Rubeni, cha Yuda, ndi cha Levi. Kuvuma, kumene kutalika kwake ndi kwa mamita 2,250, kukhale zipata zitatu: chipata cha Yosefe, cha Benjamini ndi cha Dani. Kumwera, kumene kutalika kwake ndi kwa mamita 2,250, kukhale ndi zipata zitatu: chipata cha Simeoni, cha Isakara ndi cha Zebuloni. Kuzambwe, kumene kutalika kwake ndi kwa mamita 2,250, kukhale zipata zitatu: chipata cha Gadi, cha Asere ndi cha Nafutali. Choncho kutalika kwa mzindawo kuzungulira ponse kukhale mamita 9,000, ndipo dzina la mzindawo mpaka muyaya likhale ‘Chauta-ali-pano.’ ” Pa nthaŵi ya ufumu wa Uziya, wa Yotamu, wa Ahazi ndi wa Hezekiya, mafumu a ku Yuda, ndiponso pamene Yerobowamu mwana wa Yowasi anali mfumu ya ku Israele, Chauta ankamupatsa uthenga Hoseya, mwana wa Beeri. Pamene Chauta adalankhula koyamba kudzera mwa Hoseya, adamuuza kuti, “Pita kakwatire mkazi wachiwerewere ndipo ubale naye ana omwe adzakhalenso achiwerewere. Pakuti anthu a m'dziko muno akhala osakhulupirika, pakusiya Ine Chauta.” Motero Hoseya adapita, nakakwatira mkazi, dzina lake Gomeri, mwana wa Dibulaimu. Mkaziyo adatenga pathupi, namubalira mwana wamwamuna. Tsono Chauta adauza Hoseya kuti, “Umutche dzina loti Yezireele. Pakuti patapita kanthaŵi pang'ono, ndidzalanga banja la Yehu chifukwa cha anthu amene iye adaŵapha ku Yezireele, ndipo ndidzathetsa ufumu wa Israele. Nthaŵi imeneyo ndidzathetsa mphamvu za Israele m'chigwa cha Yezireele.” Gomeri adatenganso pathupi, nabala mwana wamkazi. Chauta adauza Hoseya kuti, “Umutche dzina loti ‘Sakondedwa,’ pakuti Israele sindidzamkondanso, ndipo sindidzamkhululukiranso. Koma ndidzaonetsa chikondi kwa banja la Yuda, ndipo ndidzaŵapulumutsa ndi mphamvu zanga, Ine Chauta, Mulungu wao. Ndidzaŵapulumutsa osati pochita kumenya nkhondo ndi mauta, malupanga, akavalo ndi anthu okwera pa akavalo ai.” Sakondedwa ataleka kuyamwa, Gomeri adatenganso pena pathupi, nabala mwana winanso wamwamuna. Pamenepo Chauta adauza Hoseya kuti, “Umutche dzina loti ‘Si-anthu-anga’, pakuti inu Aisraele sindinunso anthu anga, ndipo Ine sindinenso Mulungu wanu.” Komabe Aisraele adzachuluka ngati mchenga wakunyanja umene sangathe kuuyesa kapena kuuŵerenga. Pamalo pamene Mulungu adaanena anthuwo kuti “Sindinu anthu anga,” pomweponso adzaŵatchula kuti, “Ana a Mulungu Wamoyo.” Anthu a ku Yuda ndi a ku Israele adzaŵasonkhanitsanso pamodzi, ndipo adzadzisankhira mtsogoleri mmodzi. Tsono adzatukuka m'dziko mwao, ndithu tsiku la Yezireele lidzakhala lalikulu kwambiri. Nchifukwa chake abale ako uŵauze kuti, “Ndinu anthu a Chauta”, ndiponso kuti, “Chauta wakukondani”. “Mudzudzule mai wanu, mumdzudzule pakuti salinso mkazi wanga, ndipo ine sindinenso mwamuna wake. Mumdzudzule kuti aleke kuchita chigololo, zibwenzi zake azichotse pachifuwa pake. Akapanda kutero ndimuvula, kuti akhale monga momwe adabadwira. Ndidzamuumitsa ngati chipululu, adzakhala ngati dziko lopanda madzi, ndidzamphetsa ndi ludzu. Ana ake onse sindidzaŵachitira chifundo chifukwa ndi ana am'chiwerewere. Paja mai wao ndi wachiwerewere. Amene adaŵabala ankachita zomvetsa manyazi. Ankati, ‘Nditsatira zibwenzi zanga zimene zimandipatsa chakudya ndi madzi, ubweya ndi thonje, mafuta ndi vinyo.’ “Nchifukwa chake njira yake ndidzaitseka ndi minga. Ndidzamuzinga ndi khoma, kuti asayendenso m'njira zake zakale. Adzathamangira zibwenzi zake, koma sadzapezana nazo. Adzazifunafuna, koma osazipeza. Tsono adzati, ‘Ndibwereranso kwa mwamuna wanga uja, chifukwa ndidaali pabwino ndi iyeyo kupambana tsopano.’ Sankadziŵa kuti ndine amene ndinkamupatsa tirigu, vinyo ndi mafuta. Sankadziŵa kuti ndine amene ndinkamupatsa siliva ndi golide wambiri zimene anthuwo ankapangira mafano a Baala. Nchifukwa chake ndidzamlanda tirigu wanga pa nthaŵi yodula ndi vinyo wanga pa nthaŵi yofinya. Ndidzamlandanso ubweya ndi thonje langa zimene ankavalira. Motero ndidzaonetsa dama lake poyera kwa zibwenzi zake, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adzampulumutse m'manja mwanga. Ndidzathetsa chimwemwe chake chonse, zikondwerero zake za pokhala mwezi, za masabata ndi za masiku ena onse opatulika. Ndidzaononga mitengo yake yamphesa ndi yankhuyu imene ankanena kuti, ‘Ameneŵa ndiwo malipiro anga amene zibwenzi zanga zidandipatsa.’ Ndidzaisandutsa malunje, ndipo zilombo zizidzadya kumeneko. Ndidzamlanga chifukwa choti adafukiza lubani kwa Abaala pa zikondwerero zao. Ankadzikongoletsa povala mphete ndi mikanda yamtengowapatali, kuti azithamangira zibwenzi zake, Ine nkumandiiŵala. Ndatero Ine Chauta.” “Tsono tamverani, ndidzamkopa mkaziyo, ndidzapita naye ku chipululu ndi kukamsangalatsa ndi mau achikondi. Kumeneko ndidzambwezera minda yake yamphesa. Ndidzasandutsa Chigwa cha Mavuto kuti chikhale chipata cha kuchiyembekezo. Ndipo kumeneko azidzandiyankha monga m'mene ankandiyankhira pa ubwana wake, atatuluka ku Ejipito. Nthaŵi imeneyo pondiitana uzidzati, ‘Amuna anga.’ Suzidzatinso, ‘Baala wanga.’ Ndikutero Ine Chauta. Ndidzamletsa kuti asatchulenso maina a Abaala, Ndithu anthu sadzatchulanso maina aowo popembedza. Nthaŵi imeneyo ndidzachita chipangano ndi nyama zakuthengo, mbalame zamumlengalenga, ndi zokwaŵa pansi, kuti ziyanjane ndi anthu anga. Tsono ndidzathyola uta, lupanga, ndi zida zina zonse zankhondo, ndipo ndidzazichotsa m'dzikomo, kuti iwo apeze moyo wamtendere. Iwe Israele, ndidzakutomera kuti ukhale mkazi wanga mpaka muyaya. Ndidzakutomera mwaungwiro, mwachilungamo, mwa chikondi chosasinthika, ndiponso mwachifundo. Ndidzakutomera mokhulupirika, ndipo udzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.” Chauta akunena kuti, “Nthaŵi imeneyo ndidzamvera mlengalenga, mvula idzagwa pa dziko lapansi. Nthaka idzamvera tirigu, vinyo ndi mafuta, ndipo zimenezi zidzamvera Yezireele. Israele ndidzamubzala m'dziko kuti akhale wanga. Ndidzaonetsa chikondi kwa ‘Sakondedwa’ uja. Anthu amene ndinkaŵatchula ‘Si-anthu-anga,’ ndidzaŵauza kuti, ‘Ndinu anthu anga.’ Ndipo iwo adzanena kuti, ‘Ndinu Mulungu wathu.’ ” Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Pitanso, ukakonde mkazi wachigololo amene ali ndi chibwenzi chake. Umkonde monga momwe Ine Chauta ndimakondera Israele, ngakhale iyeyo amapembedza milungu ina, ndipo amakonda kuitsirira nsembe za mphesa zabwino zoumika.” Motero ndidamkwatira popereka ndalama khumi ndi zisanu zasiliva, ndiponso mitanga isanu ndi iŵiri ya barele. Ndidamuuza mkaziyo kuti, “Uzikhala nane masiku ambiri, osachitanso zachiwerewere kapena chigololo ndi munthu wina. Nanenso ndidzachita chimodzimodzi.” Ndiye kuti Aisraele adzakhala masiku ambiri opanda mafumu kapena akalonga, osapereka nsembe kapena kuimika miyala yachipembedzo, opanda zamaula kapena mafano oombezera. Pambuyo pake Aisraelewo adzabwerera ndi kufunafuna Chauta Mulungu wao ndi mdzukulu wa Davide mfumu yao. Nthaŵi imeneyo Aisraele adzagonja kwa Chauta ndipo adzalandira zabwino zake. Inu Aisraele, imvani mau a Chauta, chifukwa Iye akukuimbani mlandu, inu anthu okhala m'dziko. Mlandu wake ndi wakuti, m'dziko mulibe kukhulupirika kapena kukoma mtima, ndipo Mulungu samulabadira. Akulumbira monama, kunena zabodza, kupha, kuba ndi kuchita chigololo. Machimo achita kunyanya, ndipo akungophanaphana. Nchifukwa chake mudzagwa chilala m'dziko, ndipo onse okhalamo adzavutika pamodzi ndi nyama zakuthengo zomwe, ndi mbalame zamumlengalenga. Ngakhale nsomba zam'nyanja zidzafa. Chauta akuti, “Wina aliyense asatsutsepo kanthu, wina aliyense asaimbe mnzake mlandu, pakuti mlandu uli pakati pa Ine ndi inu ansembe onyenganu. Mumakhumudwa usana ndi usiku, ndipo aneneri nawonso amachita chimodzimodzi, motero ndidzaononga Israele mai wanu. Anthu anga akuwonongeka chifukwa Ine sandidziŵa. Ndidzakukanani kuti musanditumikire ngati ansembe, chifukwa choti mwakana kuphunzitsa za Ine. Mwaiŵala malamulo a Mulungu wanu, tsono Inenso Mulungu wanu ndidzaiŵala ana anu. “Ansembe ankati akamachulukirachulukira, ndi m'menenso ankanyanyira kundichimwira. Ndidzasandutsa ulemu wao kuti ukhale manyazi. Amalemererapo pa kuchimwa kwa anthu anga, ndipo amafunitsitsa kuti anthuwo azichimwirachimwira. Tsono ansembewo ndidzaŵachita zomwe ndidzaŵachite anthu. Ndidzaŵalanga chifukwa cha makhalidwe ao oipa ndi kuŵalipsira pa ntchito zaozo. Azidzadya koma sadzakhuta. Azidzachita zachiwerewere, koma sadzachulukana, poti adasiya Chauta, kuti adzipereke ku zachiwerewere.” Chauta akuti, “Vinyo, kaya ndi wakale kaya ndi watsopano, amaononga nzeru. Anthu anga amapempha nzeru ku fano lamtengo, ndipo amaombeza ndi ndodo yao. Mzimu wonyansa waasokeretsa, motero posiya Mulungu wao, akhala osakhulupirika. Amapereka nsembe pa mapiri, amafukiza lubani pa zitunda, patsinde pa mitengo yogudira monga thundu, mnjale ndi mkundi, chifukwa amati mithunzi yake njabwino. “Nchifukwa chake ana anu aakazi akuchita zachiwerewere, ndipo akamwana anu akuchita zigololo. Koma sindidzaŵalanga ana anu aakazi chifukwa chochita zachiwerewere, sindidzaŵalanga akamwana anu chifukwa cha zigololo zao. Paja inu nomwe amunanu mumayenda ndi akazi achiwerewere, ndipo mumapereka nsembe pamodzi ndi akazi adama akuchipembedzo. Anthu opanda nzeru chitere adzaonongeka. “Ngakhale Aisraele amachita zosakhulupirika, anthu a ku Yuda asapezeke ndi mlandu wotere. Asapite kukapembedza ku Giligala kapena ku Betehaveni. Asakalumbirenso kumeneko kuti, ‘Pali Chauta wamoyo!’ Aisraele ndi okanika ngati anaang'ombe. Kodi Chauta angathe kuŵadyetsa tsopano ngati anaankhosa pa busa lokoma? “Anthu a ku Efuremu aphathana ndi mafano, izo nzao. Amati akamwa kwambiri, amangochita zigololo. Amakonda zamanyazi kupambana ulemu wao. Adzachotsedwa ngati chinthu chotengedwa ndi mphepo, ndipo adzachititsidwa manyazi chifukwa cha nsembe zao zachikunja.” “Ansembe inu, imvani izi! Aisraele inu, mumvetsere nonse. Inu a m'banja la mfumu, mvetserani mau anga. Chilango chidzakugwerani, chifukwa inu munali msampha ku Mizipa, mudachita ngati kuyala ukonde ku phiri la Tabori. Opandukawo azama kwambiri m'machimo ao, Ine ndidzaŵalanga onsewo. “Aefuremu ndikuŵadziŵa, Aisraele ndi osabisika kwa Ine. Aefuremu akhala osakhulupirika, Aisraele adziipitsa.” Ntchito zao zoipa zatseka njira yao yobwerera kwa Mulungu wao, pakuti mtima wa kusakhulupirika uli mwa iwo, ndipo salabadako za Chauta. Kudzikuza kwa Israele kwasanduka umboni womutsutsa. Zoonadi Efuremu adzagwa ndi machimo ake. Nayenso Yuda adzateronso. Anthu amapereka nsembe zankhosa ndi zang'ombe pofunafuna Chauta, koma samupeza, waŵachokera. Adachita zosakhulupirika kwa Chauta, motero ana ao nawonso si ake a Mulungu. Tsono chipembedzo chao chachikunja chidzaŵaonongetsa pamodzi ndi minda yao. Imbani malipenga ankhondo ku Gibea! Lizani mbetete ku Rama! Chenjezani a ku Betehaveni! Inu a ku Benjamini tsogolani! Efuremu adzasanduka bwinja pa tsiku lachilango. Ndikulengeza zoona kwa inu nonse Aisraele. Chauta akuti, “Atsogoleri a ku Yuda amachita nkhondo kuti afutuze malire. Nchifukwa chake ndidzaŵamiza ndi mkwiyo wanga ngati madzi achigumula. Aefuremu akuŵapondereza, akuŵalanga chifukwa chomvera za ena. Nchifukwa chake ndidzaononga Efuremu, monga momwe njenjete zimaonongera nsalu, ndidzakhala ngati chilonda choola pa anthu a ku Yuda. “Tsono anthu a ku Efuremu ataona kuti akudwala, ndipo Ayuda ataona kuti ali ndi mabala, Aefuremuwo adapita kwa Aasiriya, Ayuda natuma uthenga kwa mfumu yaikulu, kuti iŵathandize. Koma siingathe kuŵachiritsa kapena kupoletsa mabala ao. Ndidzalumphira Aefuremu ngati mkango, ndidzambwandira Ayuda ngati msona wa mkango. Ine mwini ndidzaŵakadzula nkuchokapo. Pamene ndizidzaŵaguza, palibe wina aliyense wotha kudzaŵalanditsa. “Ndidzabwerera ku malo anga, mpaka anthu anga atasaukiratu, ndi kuyamba kundifunafuna. M'mavuto ao adzayesetsa kundipeza.” Anthu akunena kuti, “Tiyeni, tibwerere kwa Chauta. Watikadzula, komabe adzatichiritsa. Watikantha, komabe adzamanga mabala athu. Posachedwa adzatitsitsimutsa. Patangopita masiku aŵiri kapena atatu, adzatiwukitsa kuti tikhale ndi moyo pamaso pake. Tiyeni tilimbikire kusamala za Chauta. Adzabwera kwa ife mosapeneka konse ngati mbandakucha. Kubwera kwake kudzakhala madalitso ngati mvula, mvula yake yachilimwe imene imakhathamiza nthaka.” Koma Chauta akuti, “Inu Aefuremu, kodi ndikuchiteni chiyani? Nanga inu Ayuda, ndikuchiteni chiyani? Chikondi chanu chimazimirira ngati nkhungu yam'maŵa, chili ngati mame okamuka msanga. Nchifukwa chake ndakuŵazani ngati nkhuni ndi machenjezo a aneneri, ndakuphani ndi mau anga. Chigamulo changa nchoonekeratu ngati kuŵala kwa dzuŵa. Kunena zoona Ine ndimafuna chikondi chosasinthika, osati nsembe chabe. Ndifuna kuti anthu andidziŵe Ine Mulungu m'malo mwa kumangopereka nsembe zopsereza. “Koma anthuwo adaphwanya chipangano changa monga adachitira Adamu. Potero, adandichitira zosakhulupirika. Giliyadi ndi mzinda wa anthu ochita zoipa, akungophana basi. Monga mbala zimalalira munthu, momwemonso ansembe amasonkhana kuti azipha anthu pa njira ya ku Sekemu. Zoonadi amachita zachifwamba zambiri. Pakati pa Aisraele ndaonapo zinthu zonyansa. Aefuremu adachita zadama, Aisraele adadziipitsa pakupembedza mafano. “Inunso Ayuda mudzakolola chilango. Ndikati ndibwezere anthu anga pabwino, ndikati ndichiritse Aisraele, uchimo wao umaonekera poyera. Ntchito zoipa za anthu a ku Samariyawo sizibisika ai. Sakhulupirika, amanyenga anthu, amathyola nyumba ngati mbala, ndi achifwamba, amalandanso zinthu za anthu poyera. Koma saganiza kuti Ine sindiiŵala ntchito zao zoipa. Zolakwa zao zaŵazinga, ndipo sizichoka m'maso mwanga.” Anthu amakopa mfumu ndi makhalidwe ao oipa, nduna zake amazinyenga ndi mabodza ao. Onsewo ndi osakhulupirika, udani wao ndi wonyeka ngati moto wamuuvuni, umene mphikabuledi sasonkhezera kuyambira pamene akukanyanga mtanda wa buledi mpaka utafufuma. Pa tsiku la chikondwerero cha mfumu, nduna zake zimadakwa, mfumu nkuloŵa nawo m'gulu la anthu oipanganirana. Mitima yao imatentha ngati uvuni ndi upo wao. Usiku wonse, ukali wao umanyeka, ndipo m'maŵa umayaka ngati moto. Onsewo amakhala juu ngati uvuni, ndipo amapha olamulira ao. Imodziimodzi mafumu ao onse agwa, koma palibe ndi mmodzi yemwe wondiitana. Chauta akuti, “Aefuremu ali ngati keke yopsa kumodzi, chifukwa amasakanizikana ndi anthu a mitundu ina. Alendowo akuŵatha mphamvu, iwo osadziŵako. Akuyamba kumera imvi, iwo osadziŵako. Aisraele kunyada kwao komwe kukuŵatsutsa. Koma pa zonsezi sakubwerera kwa Chauta Mulungu wao, sakumfunafuna konse. “Aefuremu ali ngati nkhunda yopusa, yopanda nzeru. Amaitana Aejipito, namapita ku Asiriya kukapempha chithandizo. Kulikonse kumene amapita, ndidzaŵatchera ukonde. Ndidzaŵagwetsa pansi ngati mbalame zamumlengalenga. Ndidzaŵalanga chifukwa cha zolakwa zao. “Tsoka kwa iwo pakuti andisiya Ine. Aonongeke chifukwa chakuti andipandukira. Ndimafuna kuŵapulumutsa, koma amangolankhula zabodza za Ine. Kulira kwao kwa Ine nkwabodza, amalira ali gone pa bedi. Amadzichekacheka ngati akunja chifukwa chofuna chakudya ndi chakumwa, komabe amandipandukira. Ngakhale ndimaŵalera ndi kuŵalimbitsa, komabe amandichita zachiwembu. Amatembenukira kwa mulungu wachabechabe, osati kwa Mulungu wopambanazonse. Ali ngati uta wokhota. Atsogoleri ao adzaphedwa ndi lupanga chifukwa chakuti amandilankhulira zachipongwe. Motero a ku Ejipito adzaŵaseka kwambiri.” Chauta akuti, “Lizani lipenga! Adani akugudukira dziko la Chauta ngati adembo pamwamba pa nyama. Anthu anga aphwanya chipangano changa, ndipo achimwira malamulo anga. Amalirira kwa Ine kuti ndiŵathandize, amati, ‘Ife Aisraele tikukudziŵani Inu Mulungu wathu.’ Koma Aisraele akana zabwino. Nchifukwa chake adani ao adzaŵapirikitsa. “Amadzilongera mafumu mosatsata kufuna kwanga. Amadziikira atsogoleri popanda chilolezo changa. Adzipangira mafano asiliva ndi agolide, koma adziwononga nawo. Fano la mwanawang'ombe limene a ku Samariya akupembedza likundinyansa. Motero mkwiyo wanga waŵayakira kwambiri anthuwo. Padzapita nthaŵi yaitali chotani asanasinthe kuti ayere anthu a ku Israele? “Fanolo si mulungu konse, adalipanga ndi munthu waluso. Fano la ku Samariyali lidzatswanyidwa pafupipafupi. “Aisraele amafesa kamphepo, ndipo amakolola kamvulumvulu. Tirigu alibe ngala, sadzabala chakudya. Akadabala, alendo akadadya chakudyacho. Aisraele amezedwa. Asanduka ngati chiŵiya chachabe pakati pa anthu a mitundu ina. Adathaŵira ku Asiriya ngati mbidzi yongodziyendera payokha. Aefuremu adalipira anthu a ku maiko ena kuti akhale oŵathandiza. Chifukwa choti adagwirizana ndi anthu a mitundu ina, ndidzaŵasonkhanitsa ndi kuŵaononga. Posachedwa adzazunzika kwambiri chifukwa cha ulamuliro wa mfumu ya ku Asiriya. “Aefuremu adachulukitsa maguwa ansembe ochotserapo machimo, koma maguwawo asanduka malo ochimwirapo. Ndidaŵapatsa malamulo ambiri olembedwa, koma saŵasamala. Amaŵayesa achilendo. Amapereka nsembe zanyama kwa Ine nkumadya, koma Ine Chauta sindikondwera nazo konse. Sindidzaiŵala zolakwa zao, ndidzaŵalanga chifukwa cha zimenezo. Ndidzaŵabwezera ku ukapolo ku Ejipito. Aisraele adzimangira nyumba zikuluzikulu, kuiŵala Mlengi wao. Ayuda achulukitsa mizinda yamalinga. Koma Ine ndidzaponya moto pa mizinda yaoyo, ndipo motowo udzatentha nyumba zao zazikuluzo.” Musakondwere Aisraele inu! Musakhale ndi chisangalalo chonga cha mitundu ina ya anthu. Mwasiya Mulungu wanu monga amachitira mkazi wosakhulupirika. Mwadzigulitsa kwa Baala ngati mkazi wadama, kuti mukalandireko zokolola zambiri. Tirigu ndi mphesa simudzakhala nazo zokwanira. Mudzasoŵanso vinyo woti muzimwa. Simudzakhalanso m'dziko la Chauta. Aefuremu inu, mudzabwerera ku ukapolo ku Ejipito, mudzadya chakudya choletsedwa ku dziko la Asiriya. Kumeneko anthu sadzaperekanso zopereka za chakumwa kupereka kwa Chauta. Sadzamkondwetsanso ndi nsembe zao. Chakudya chao chidzakhala ngati chakudya chapamaliro, onse amene adzadya chakudya chimenecho adzaipitsidwa. Chakudyacho chidzangokhala chodyera njala chabe, osati choti nkukapereka ku Nyumba ya Chauta. Kodi pa tsiku la chikondwerero, tsiku lolemekeza Chauta, anthuwo adzachitapo chiyani? Nthaŵi ya chilango ikadzafika, iwo nkubalalika, Aejipito adzaŵakusa, nakaŵaika m'manda komweko ku Memfisi. Khwisa adzamera pa ziŵiya zao zasiliva. M'nyumba mwao mudzamera minga. Nthaŵi ya chilango yafikadi, masiku olipsira aŵagwera. Pamenepo adzadziŵa kuti zimenezi nzoonadi. Tsopano akunena kuti, “Mneneriyu nchitsilu, munthu wa nzeru za kwa Mulunguyu ndi wamsala!” Amatero chifukwa zolakwa zao zachuluka, chidani chao nchachikulukulu. Mneneri ndiye wochenjeza Aefuremu, anthu a Mulungu wanga. Koma mneneriyo amtchera msampha m'njira zake zonse, ndipo adani akumlalira m'Nyumba ya Mulungu. Anthu aipiratu monga zidachitikira ku Gibea. Nchifukwa chake Mulungu sadzaiŵala kuipa kwao, ndipo adzalanga machimo ao. Chauta akuti, “Israele ndidampeza ngati mphesa zam'thengo. Makolo ake aja ndidaŵakondwerera ngati nkhuyu zoyamba kupsa. Koma iwowo adapita kwa Baala-Peori, ndipo kumeneko adadzipereka kwa Baala. Motero adasanduka chinthu chonyansa ngati fano laolo, limene ankalikonda lija. Ulemerero wa Aefuremu udzaŵathaŵa mouluka ngati mbalame. Sadzabalanso ana. Akazi ao sadzaima, sadzatenga pathupi. Ngakhale abale ana, ndidzaŵaononga, sadzakhalapo ndi mmodzi yemwe. Tsoka kwa anthuwo ndikadzaŵasiya.” Inu Chauta, monga ndikuwonera, ana a Efuremu adzakhala ngati nyama zojiwa. Aefuremu adzatsogolera ana ao kunkhondo kumene adzaphedwe. Muŵapatse, Inu Chauta. Kodi mudzaŵapatse chiyani? Muŵapatse mimba yopita padera ndi maŵere ouma! Chauta akuti, “Kuipa kwao konse kudaoneka makamaka ku Giligala. Ndidayamba kudana nawo kumeneko. Ndidzaŵapirikitsa m'dziko mwanga, chifukwa makhalidwe ao ndi oipa. Sindidzaŵakondanso, atsogoleri ao onse andiwukira. Efuremu ali ngati mtengo wodulidwa umene mizu yake yauma, ndipo sudzabalanso zipatso. Ngakhale anthuwo abale ana, ndidzaŵapha ana ao okondedwawo.” Mulungu wanga adzaŵataya anthu amenewo chifukwa choti sadamumvere. Adzasanduka oyendayenda pakati pa mitundu ya pa dziko lapansi. Aisraele ali ngati mpesa wokondwa umene unkabala zipatso zambiri. Chuma chao chikamanka chichuluka, chipembedzo chachikunja chinkakulirakuliranso. Dziko lao likamanka litukuka, iwo ankakometserakometsera mafano ao amene ankaŵapembedza. Mtima wao ndi wonyenga. Tsopano ayenera kulangidwa chifukwa cha machimo ao. Chauta adzagumula maguwa ao ansembe, ndipo adzaononga miyala yao yoimiritsa yachipembedzo. Posachedwa anthuwo adzanena kuti, “Tilibe mfumu tsopano chifukwa sitidamvere Chauta. Komabe mfumuyo ikadatichitira chiyani ife?” Mafumu akungolankhula mau opandapake. Amangochita zipangano ndi malonjezo abodza. Chilungamo chasanduka kusalungama kumene kumaphuka ngati udzu woipa m'munda. Anthu a ku Samariya adzachita mantha, fano la mwanawang'ombe la ku Betehaveni likadzaonongedwa. Anthu ake adzalirira. Nawonso ansembe ake aja adzalira maliro a mulungu waoyo, chifukwa ulemerero wake wonse wachokeratu. Zoonadi, fanolo lidzatengedwa kupita ku Asiriya, kuti likakhale mphatso yoperekedwa kwa mfumu yaikulu. Aefuremu adzachita manyazi, Aisraelewo adzachita manyazi chifukwa cha malangizo onama amene ankamvera. Mfumu ya ku Samariya idzatengedwa kunka kutali ngati kanthambi koyenda pa madzi. Akachisi opembedzerako milungu yabodza amene Aisraele ankachimwirako, idzaonongedwa. Minga ndi mitungwi zidzamera pa maguwawo. Anthu adzauza mapiri kuti, “Tigwereni!” Adzauza magomo kuti, “Tipsinjeni!” Chauta akuti, “Kuyambira uchimo wa ku Gibea, Aisraele akhala akuchimwabe. Motero adzagonjetsedwa pa nkhondo ku Gibea komweko. Ndidzabwera kudzalimbana ndi anthu aupanduŵa kuti ndiŵalange. Anthu a mitundu ina adzasonkhana kuti aŵathire nkhondo chifukwa cha uchimo wao waukulu. Kale Efuremu anali ngati ng'ombe yophunzitsidwa imene inkakonda kupuntha tirigu. Tsopano m'khosi lake lokongola ndaikamo goli, kuti agwire ntchito koposa. Ndifuna kuti Yuda azitipula, Yakobe azimwanya mauma. Mudzifesere m'chilungamo, ndipo mudzakolola madalitso a chikondi changa chosasinthika. Tipulani tsala lanu pakuti nthaŵi yofunafuna Chauta yakwana. Funafunani Chautayo mpaka atabwera kudzakugwetserani mvula ya madalitso. Mudabzala zolakwa, ndipo mudakolola chilango chake. Mwadya zotsatira zake za mabodza. Chifukwa choti mwadalira magaleta anu, ndi kuchuluka kwa anthu anu a nkhondo, adani anu adzakuthirani nkhondo. Malinga anu onse adzaonongedwa monga momwe Salamani adaonongera Betaribele pa tsiku la nkhondo. Adaphwanya azimai pamodzi ndi ana omwe. Momwemo zidzakuchitikirani inu a ku Betele chifukwa cha uchimo wanu waukulu. Nkhondo ikadzangoyamba m'mamaŵa, nayonso mfumu ya ku Israele idzaphedwa.” Chauta akuti, “Pamene Israele anali mwana, ndinkamukonda. Mwana wangayo ndidamuitana kuti atuluke ku Ejipito. Ine ndikamakangaza kumuitana, iye ndiye kumandithaŵa kunka kutali. Ankaperekabe nsembe kwa Baala ndi kulitenthera lubani fanolo. Komabe ndine amene ndidaphunzitsa Aefuremu kuyenda. Ndidaŵalera, koma sadavomereze kuti amene ndidaŵasamala ndine. Ndidaŵakokera kwa Ine mwachifundo ndi mwachikondi. Ndidaŵanyamula nkuŵatsamiza kutsaya kwanga. Ndidaŵerama, nkuŵadyetsa. “Tsono anthuwo adzabwereranso ku ukapolo ku Ejipito. Aasiriya adzakhala oŵalamulira, pakuti iwo akana kubwerera kwa Ine. Nkhondo idzaononga mizinda yao. Adani adzaphwanya zipata za malinga ao ndi kuŵaononga, chifukwa chotsata nzeru zaokha. Anthu anga akangamira zondipandukira Ine. Tsono adzalira chifukwa cha goli lachilango limene lili pa iwo, koma palibe amene adzaŵachotsere. “Kodi ndingakusiye bwanji iwe Efuremu? Kodi ndingathe kukutaya bwanji iwe Israele? Kodi ndingathe bwanji kukusandutsa ngati Adima? Kodi ndingathe kukuwononga ngati Zeboimu? Mtima wanga wakana kutero, chifundo changa chikukula. Sindidzalekerera kuti mkwiyo wanga ukulangitse, sindidzamuwononganso Efuremu, pakuti Ine ndine Mulungu osati munthu. Ine, Woyera uja, ndili nawe, ndipo sindidzabwera kudzakuwononga. “Ndidzaŵabangulira ngati mkango, ndipo anthu anga adzanditsata. Ndidzabanguladi, ndipo adzathamangira kwa Ine ali njenjenje kuchokera kuzambwe. Adzabwera akunjenjemera ngati mbalame kuchokera ku Ejipito, adzabwera ngati njiŵa kuchokera ku Asiriya. Motero ndidzaŵabwezeranso kwao. Ndikutero Ine Chauta.” Chauta akuti, “Anthu a ku Efuremu andizinga ndi mabodza. Banja limeneli la Israele nlonama kwambiri. Nawonso anthu a ku Yuda akundipandukirabe Ine Mulungu, Woyera ndi wokhulupirika. Efuremu chakudya chake ndi mpweya wokhawokha. Amanka nasaka mphepo yakuvuma tsiku lonse. Amachulukitsa mabodza ndi chiwawa. Amachita chipangano ndi dziko la Asiriya, ndipo amapereka mitulo ya mafuta ku Ejipito.” Chauta akuŵaimba mlandu anthu a ku Yuda. Adzalanga a m'banja la Yakobe chifukwa cha makhalidwe ao, adzaŵabwezera zolingana ndi ntchito zao zoipa. Akali m'mimba mwa mai wake, Yakobe adakangana ndi mbale wake, ndipo atakula adalimbana ndi Mulungu. Yakobeyo adalimbana ndi mngelo ndipo adapambana. Adalira napempha madalitso. Mulungu adakumana naye ku Betele, ndipo kumeneko podzera mwa iyeyo adalankhula nafe. Ameneyu ndiye Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse. Anthu azimkumbukira ndi dzina lakeli loti Chauta. Motero bwererani nonsenu ndi chithandizo cha Mulungu wanu. Mukhale achikondi ndi olungama, ndipo muzidalira Mulungu wanu nthaŵi zonse. Chauta akuti, “Aisraele ali ngati wamalonda wonyenga amene amagwiritsa ntchito masikelo onama. Amakonda kumeta anthu. Aefuremu akunena kuti, ‘Ndithu talemera, takhuphuka zedi, wina sangatiloze chala pa kulemera kumeneku.’ Koma Ine ndine Chauta, Mulungu wanu, amene ndidakutulutsani ku Ejipito. Ndidzakukhalitsaninso m'mahema, monga munkachitira masiku amakedzana m'chipululu muja. Ndidalankhula ndi aneneri. Ndine amene ndidaŵaonetsa zinthu zambiri ngati kutulo. Ndidalankhula m'mafanizo kudzera mwa iwo. Komabe anthu ankapembedza mafano ku Giliyadi. Ndithu mafano ameneŵa adzaonongedwa. Ankapereka nsembe za nkhunzi ku Giligala, koma maguwa ansembewo ndidzaŵasandutsa miyulu ya miyala m'munda.” (Yakobe adathaŵira ku dziko la Aramu. Israeleyo adagwira ntchito kumeneko kuti apeze mkazi. Ankaŵeta nkhosa kuti akwatire mkaziyo). Chauta adatulutsa Aisraele ku Ejipito kudzera mwa mneneri. Ndipo mwa mneneriyo adaŵasungabe. Koma Aefuremuwo adaputa mkwiyo wake, nchifukwa chake Chauta adzaŵalanga ndi imfa. Adzaŵalanga chifukwa adamchititsa manyazi kwambiri. Kale Aefuremu ankati akalankhula, anthu ankachita mantha chifukwa ankalemekezeka m'dziko la Israele, koma adalakwa popembedza Baala, motero adzafa. Masiku ano akuchimwirachimwira. Akudzipangira mafano oumba pogwiritsa ntchito siliva wao. Mafano onsewo ndi ntchito ya anthu aluso. Amati, “Perekani nsembe kwa ameneŵa, pembedzani anaang'ombeŵa poŵampsompsona.” Nchifukwa chake adzazimirira ngati nkhungu yam'maŵa, kapena mame okamuka msanga. Adzamwazika ngati mungu wouluzika kuchokera pa malo opunthira tirigu, kapena ngati utsi wotuluka pa zenera. Chauta akuti “Ine ndakhala Chauta Mulungu wako kuyambira nthaŵi imene ndidakutulutsa ku Ejipito. Sudziŵa Mulungu wina, koma Ine ndekha, Mpulumutsi wako ndine ndekha. Ndine ndidakusamalani m'chipululu, m'dziko lotentha kwambiri. Ndidaŵadyetsa, nakhuta, koma atakhuta, adanyada, ndipo adandiiŵala Ine. Motero ndidzaŵalumphira ngati mkango, ndidzaŵalalira ngati kambuku m'mbali mwa njira. Ndidzaŵambwandira ngati chimbalangondo cholandidwa ana. Ndidzathyola nthiti zao, ndipo ndidzaŵamwamwata pomwepo ngati mkango, ndidzaŵankhanthula ngati chilombo choopsa. “Ndidzaononga inu Aisraele. Kodi ndani angakuthandizeni? Inu munkati, ‘Tipatseni mfumu ndi atsogoleri.’ Nanga tsopano mfumu yanuyo, yoti ikulanditseni, ili kuti? Nanga atsogoleri anuwo, oti akutchinjirizeni, ali kuti? Ndidakupatsani mafumu mwachipsera mtima. Kenaka atandikwiyitsa, ndidaŵachotsa. “Kuipa kwa anthu a ku Efuremu kwalembedwa m'buku, buku lake la machimo ao ndalisunga. Zoŵaŵa zonga za mkazi pobala mwana zidzaŵagwera. Akadapulumutsidwa, koma ali ngati mwana wopanda nzeru, wosafuna kutuluka pa nthaŵi yake yobadwa. Kodi ngati ndidzaŵapulumutsa kwa akufa? Kodi ngati ndidzaŵaombola ku imfa? Kodi iwe imfa, miliri yako ili kuti? Kodi iwe manda, kuwononga kwako kuli kuti? Anthu ameneŵa sindidzaŵachitiranso chifundo. Ngakhale kuti Efuremu akondwe ngati bango, mphepo yakuvuma mphepo ya Chauta, idzakuntha kuchokera kuchipululu. Motero kasupe wake adzaphwa, ndipo chitsime chake chidzauma. Adani adzaononga chuma chake chamtengowapatali. A ku Samariya adzalangidwa chifukwa choti adapandukira Mulungu wao. Adzaphedwa ndi lupanga, ana ao adzaphedwa moŵakankhanthitsa pansi. Akazi ake apathupi adzang'ambidwa.” Inu Aisraele, bwererani kwa Chauta, Mulungu wanu, pakuti mwagwa chifukwa cha machimo anu, Bwererani kwa Chauta, ndipo mumpemphe kuti, “Mutikhululukire machimo athu onse. Mumvere pempho lathu ndipo tidzakuyamikani ndi mau otamanda. Aasiriya sadzatipulumutsa, akavalo ankhondo sadzatiteteza. Chimene tidapanga ndi manja athu sitidzachitchulanso kuti, ‘Mulungu wathu,’ pakuti ndinu amene mumachitira chifundo amasiye.” Chauta akuti, “Ndidzachiza matenda ao a kusakhulupirika. Ndidzaŵakonda kwambiri, pakuti ndaleka kuŵakwiyira. Ndidzatsitsimutsa Israele ngati mame. Adzachita maluŵa ngati kakombo, adzazika mizu ngati mtengo wa ku Lebanoni. Ziphukira zake zidzatambasukira kutali, adzakhala wokongola ngati mtengo wa olivi, adzakhala wonunkhira ngati mkungudza wa ku Lebanoni. Aisraele adzapezanso chitetezo mwa Ine. Adzakolola tirigu wambiri, adzachuluka ngati mphesa. Adzakhala otchuka ngati vinyo wa ku Lebanoni. Kodi Aefuremu adzachita nawonso chiyani mafano? Ndine amene ndimamva pemphero lao ndi kuŵasamala. Ndili ngati mkungudza wogudira nthaŵi zonse, ndine amene ndimaŵapatsa zipatso.” Amene ali wanzeru amvetse zimenezi. Amene ali womvetsa, azisunge. Pakuti njira za Chauta nzolungama, ndipo olungama amayendamo, koma ochimwa amakhumudwamo. Nawu uthenga umene Chauta adapatsa Yowele, mwana wa Petuwele: Inu akuluakulu, mverani. Tcherani khutu, inu nonse okhala m'dziko. Kodi zoterezi zidaonekapo nthaŵi yanu kapena nthaŵi ya makolo anu? Muŵauze ana anu, iwowo auze ana ao, ndipo anawo aziwuzanso ana ao. Chimene chiwala chidasiya, dzombe lidadya. Chimene dzombe lidasiya, mandowa adadya, chimene mandowa adasiya, chilimamine adadya. Dzukani inu zidakwa, ndipo mulire. Mulire modandaula inu nonse okonda vinyo: mphesa zotchezera vinyo watsopano zaonongedwa, Chikhamu cha dzombe chagwa m'dziko lathu nchamphamvu ndiponso chosaŵerengeka. Mano ake ali ngati a mkango wamphongo, zibwano zake ngati za mkango waukazi. Aononga mpesa wanga, athyolathyola mitengo yanga ya mikuyu. Aisadza, aikungunula makungwa, naŵataya, nthambi zake nkumazisiya zili mbee. Inu anthu, lirani kwambiri ngati namwali wovala chiguduli. Wolira chifukwa cha imfa ya mnyamata wofuna kumkwatira. Chopereka cha chakumwa ndi cha chakudya siziperekedwanso ku Nyumba ya Chauta. Ansembe akulira, atumiki a Chauta aja. Minda yaguga, nthaka ikulira poti tirigu waonongeka, mphesa zaumiratu, mitengo ya mafuta yauma. Tayani mtima, inu alimi, lirani, inu olima mphesa, chifukwa tirigu ndi barele, ndi zonse zam'minda zalephera. Mpesa wauma, mkuyu wafota. Mkangaza, kanjedza, mitengo ya apulosi ndi mitengo yonse ya m'dziko yaumiratu. Choncho chikondwerero cha anthu chatheratu. Inu ansembe, valani ziguduli mudzigunde pa chifuwa chifukwa cha chisoni. Lirani, inu otumikira ku guwa. Tiyeni, mufunde ziguduli usiku wonse, inu atumiki a Mulungu wanga. Pakuti chopereka cha chakudya ndi chakumwa sizidzaonekanso ku Nyumba ya Mulungu wanu. Lamulani kuti anthu asale zakudya. Itanitsani msonkhano waulemu. Akulu ndi onse okhala m'dziko asonkhane ku Nyumba ya Chauta, Mulungu wanu, ndipo iwowo alire kwa Iye. Kalanga ine! Tsiku loopsa layandikira, tsiku la Chauta, likubwera ndi chiwonongeko chochokera kwa Mphambe. Chakudya chathu chikutha ife tikuwona. Mulibenso chimwemwe ndi chisangalalo m'Nyumba ya Mulungu wathu. Mbeu zakongonyala, poti pansi mpouma. Nyumba zosungiramo dzinthu zaonongeka, nkhokwe zapasuka, popeza kuti zokolola palibe. Zoŵeta zikulira ndi njala. Ng'ombe zikungoyenda uku ndi uku chifukwa choti zilibe busa. Nazonso nkhosa zikusauka. Ndikulira kwa Inu Chauta, pakuti moto wapsereza mabusa akuthengo, ndipo malaŵi a moto apsereza mitengo yonse yam'tchire. Nazonso nyama zakuthengo zikulira kwa Inu, chifukwa timitsinje tonse taphwa, ndipo moto wapsereza mabusa akuthengo. Lizani lipenga ku Ziyoni. Fuulani mochenjeza pa phiri langa loyera. Onse okhala m'dziko anjenjemere, pakuti tsiku la Chauta likufika, layandikira. Ndi tsiku lamdima ndi lachisoni, tsiku lamitambo ndi la mdima wandiweyani. Gulu la ankhondo amphamvu ochuluka langoti bii ngati mdima wokuta mapiri. Gulu lotere silinaonekepo nkale lonse, ngakhale kutsogolo kuno silidzaonekanso. Kutsogolo kwake moto ukupsereza, kumbuyo kwake malaŵi a moto akutentha zinthu. Iwo asanafike, dziko linali ngati munda wa Edeni, koma atachoka, lidasanduka chipululu! Palibe kanthu kotsalapo. Maonekedwe ake ali ngati a akavalo, liŵiro lake ngati la akavalo ankhondo. Akulumpha pamwamba pa mapiri ndi phokoso longa la magaleta. Akumveka ngati malaŵi a moto otentha ziputu, ngati gulu lamphamvu lankhondo litakonzekera kumenya nkhondo. Anthu a mitundu ina amachita mantha akaŵaona, nkhope zonse zimatumbuluka. Akududuka ngati ankhondo. Akukwera malinga ngati asilikali. Aliyense akuyenda pa mzere, osasempha njira yake. Sakukankhanakankhana, aliyense akuyenda molunjika. Akupyola pakati pa zida zankhondo, osaŵaimitsa. Akuulumphira mzindawo, akukwera pamwamba pa malinga. Akuloŵa m'nyumba, akuloŵera pa windo ngati mbala. Dziko lapansi likugwedezeka pamene iwo akuyandikira. Mlengalenga ukunjenjemera. Dzuŵa ndi mwezi zikuchita mdima, ndipo nyenyezi zikuleka kuŵala. Chauta akumveketsa liwu lake kutsogolo kwa gulu lake lankhondo. Gulu lake lankhondolo ndi lalikulu kwambiri. Wochitadi zimene Chauta akulamula, ngwamphamvu. Tsiku la Chauta ndi lalikulu ndi loopsa. Ndani angathe kupirira tsikulo? Koma Chauta akunena kuti, “Ngakhale tsopano bwererani kwa Ine ndi mtima wanu wonse, mukusala zakudya, mukukhetsa misozi ndi kulira mwachisoni. Ng'ambani mitima yanu, osati zovala zanu chabe.” Bwererani kwa Chauta, Mulungu wanu, poti Iye ngwokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wa chikondi chosasinthika. Nthaŵi zonse ndi wokonzeka kukhululuka. Mwina mwake adzasintha mtima ndi kuleka, ndipo adzatisiyira madalitso. Madalitsowo adzakhala a chopereka cha chakudya ndi chakumwa zopereka kwa Chauta, Mulungu wanu. Lizani lipenga ku Ziyoni. Lengezani mwambo wa kusala zakudya. Muitanitse msonkhano waukulu. Sonkhanitsani anthu pamodzi, muŵauze kuti adziyeretse. Sonkhanitsani akuluakulu, sonkhanitsani ana, sonkhanitsani ndi oyamwa omwe. Lamulani kuti nawonso akwati achoke m'chipinda mwao, abwere. Ansembe, amene ali atumiki a Chauta, azilira pakati pa guwa lansembe ndi khonde. Azinena kuti, “Inu Chauta, achitireni chifundo anthu anu. Musalole kuti ena aŵanyoze anthu anu osankhidwa. Anthu achikunja asaŵaseke pomafunsana kuti, ‘Ha, ali kuti Mulungu waoyo?’ ” Apo chikondi cha Chauta chidayaka ngati moto chifukwa cha dziko lake, ndipo adaŵachitira chifundo anthu ake. Chauta adaŵayankha anthu ake kuti, “Ndikutumizirani tirigu, vinyo ndi mafuta, ndipo mudzakhuta ndithu. Sindidzalolanso kuti akunja akunyozeni. Ndidzachotsa adani akumpoto kuti akhale kutali ndi inu, ndipo ndidzaŵapirikitsira ku dziko louma ndi lachipululu. Akutsogolo ndidzaŵathamangitsira ku nyanja yakuvuma, akumbuyo ndidzaŵathamangitsira ku nyanja yakuzambwe. Tsono mitembo yao idzatulutsa chivundi ndi fungo lonunkha. Zoonadi Chauta adachita zazikulu. “Iwe dziko, usachite mantha. Kondwa ndipo usangalale, pakuti Chauta mwini wake adachita zazikulu. Inu nyama zakuthengo, musaope, pakuti msipu wakuchipululu akuphukira. Mitengo ikubala zipatso. Mkuyu ndi mpesa zikubereka kwamphamvu. “Inu anthu a ku Ziyoni, kondwani ndi kusangalala chifukwa cha zimene Chauta, Mulungu wanu, wakuchitirani. Wakukomerani mtima pokupatsani mvula mofulumira. Wakupatsani mvula yochuluka, kumayambiriro ndi kumathero, monga pa masiku amekedzana. “Pa malo opunthira padzadzaza tirigu. Mopondera mphesa mudzasefukira vinyo watsopano, mafutanso adzachuluka. Motero ndidzakubwezerani zonse zimene zidaonongedwa ndi dzombe, mandowa, mphutsi ndi ziwala. Limenelitu ndiye gulu lankhondo lija limene ndidatuma kudzakukanthani. “Mudzadya zambiri ndi kukhuta, ndipo mudzatamanda dzina la Chauta, Mulungu wanu, amene wakuchitirani zodabwitsa. Choncho anthu anga sadzaŵanyozanso ai. Mudzadziŵa kuti Ine ndili naye Israele, ndipo kuti Ine ndekha, osati wina, ndine Chauta, Mulungu wanu. Anthu anga sadzaŵanyozanso ai. “Patapita nthaŵi, tsiku lidzafika pamene ndidzatsitsa mzimu wanga pa mtundu uliwonse wa anthu. Ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzalosa. Nkhalamba zanu zidzalota maloto, ndipo achinyamata anu adzaona zinthu m'masomphenya. Masiku amenewo, ndidzatsitsa mzimu wanga ngakhale pa akapolo ndi pa adzakazi omwe. “Mu mlengalenga ndi pa dziko lapansi ndidzaonetsa zodabwitsa izi: magazi, moto ndi utsi watoloo. Dzuŵa lidzasanduka mdima, ndipo mwezi udzasanduka magazi, tsiku lalikulu ndi loopsa la Chauta lisanafike. Ndipo aliyense amene adzatama dzina la Chauta mopemba, adzapulumuka. Monga Iye adanenera, kudzakhala ena opulumuka ku phiri la Ziyoni ndi ku Yerusalemu, ndipo mwa otsalawo padzapezeka ena amene Chauta adzaŵaitana. “Nthaŵi imeneyo itafika, masiku amene ndidzakwezanso anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu, ndidzasonkhanitsa pamodzi anthu a mitundu yonse, ndipo ndidzaŵatengera ku chigwa cha Yehosafati. Kumeneko ndidzaŵaweruza chifukwa cha zimene adachitira Aisraele, osankhidwa anga, pakuti adaŵamwaza m'maiko ao onse, nagaŵana dziko langa. Adagaŵana anthu anga pochita maere, mnyamata adamsinthitsa ndi mkazi wadama, mtsikana nkumsinthitsa ndi vinyo, kenaka adamumwa vinyoyo. “Kodi inu a ku Tiro, a ku Sidoni ndi a ku madera a Filistiya, mukuti mundichite chiyani? Kodi mumati mundilipsirire chifukwa cha zina zimene ine ndakuchitani? Ngati pali kanthu koti mundilipsirire, ndidzabwezera zochita zanu zonse pamutu panu mofulumira. Inu mudatenga siliva ndi golide wanga ndi zinthu zanga zina zamtengowapatali, kupita nazo ku nyumba za milungu yanu. Mudakagulitsa anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kwa Agriki, kuti mupite nawo kutali ndi malire a dziko lao. Koma ndidzaŵadzutsa kuti achoke kumalo kumene mudaŵagulitsa. Kenaka ndidzabwezera zochita zanu zonse pamutu panu. Ndidzagulitsa ana anu aamuna ndi aakazi kwa anthu a ku Yuda, ndipo iwo adzaŵagulitsa kwa Aseba, mtundu wa anthu okhala kutali aja. Ndatero Ine Chauta. “Mulengeze pakati pa anthu a mitundu ina kuti, ‘Konzekerani nkhondo, itanani ankhondo amphamvu. Asilikali onse afike pafupi, ayambe nkhondo. Sulani makasu anu kuti akhale malupanga. Sulani migwandali yanu kuti ikhale mikondo. Ngakhale wofooka anene kuti, Ndalimba mtima. “ ‘Fulumirani, bwerani, inu anthu a mitundu yonse yozungulira, ndipo musonkhane kumeneko.’ ” Inu Chauta, tumizani ankhondo anu. “Anthu a mitundu yonse akonzeke ndipo abwere ku chigwa cha Yehosafati. Pakuti kumeneko ndidzaweruza anthu a mitundu yonse, ochokera ku mbali zonse. “Samulani zenga wodulira tirigu, pakuti mbeu zacha kale kudikira kholola. Bwerani, dzapondeni mphesa, poti mopondera mphesa mwadzaza, ndipo mbiya zikusefukira. Chonchonso zolakwa za mitundu ina ya anthu zachuluka zedi.” Makamu ndi makamu a anthu ali m'Chigwa cha Chiweruzo. Ndithu tsiku la Chauta layandikira m'Chigwa cha Chiweruzo. Dzuŵa ndi mwezi zada, ndipo nyenyezi zaleka kuŵala. Chauta akukhuluma ku Ziyoni, mau ake amveka ngati bingu kuchokera ku Yerusalemu. Ndipo thambo ndi dziko lapansi zikugwedezeka. Koma Chauta ndiye pothaŵirapo anthu ake, ndiye linga lotetezera a ku Israele. “Motero mudzadziŵa kuti ndine Chauta, Mulungu wanu, amene ndimakhala ku Ziyoni, ku phiri langa loyera. Yerusalemu adzakhala woyera ndipo alendo sadzamthiranso nkhondo. “Nthaŵi imeneyo ikadzafika, mapiri adzakhetsa vinyo watsopano, ndipo kuzitunda kudzayenderera mkaka. Mitsinje yonse ya ku Yuda idzadzaza ndi madzi. Kasupe adzatumphuka ku Nyumba ya Chauta ndi kuthirira chigwa cha Sitimu. “Koma Ejipito adzasanduka chipululu, ndipo Edomu adzakhala bwinja lopanda anthu, chifukwa cha nkhondo imene adathira pa anthu a ku Yuda ndiponso chifukwa cha kukhetsa magazi a anthu osalakwa ku dziko lao. Koma ku Yudako kudzakhala anthu mpaka muyaya, ndipo ku Yerusalemu sikudzatha anthu pa mibadwo yonse. Ndidzalipsira magazi a ophedwawo, sindidzalekerera tchimo la olakwawo. Ine Chauta ndimakhala ku Ziyoni.” Naŵa mau a Amosi amene ankaŵeta nkhosa ku Tekowa. Zimenezi, zodzachitikira Aisraele, Chauta adamuululira pa nthaŵi ya Uziya, mfumu ya ku Yuda, ndi pa nthaŵi ya Yerobowamu, mwana wa Yowasi, mfumu ya ku Israele, kutatsala zaka ziŵiri kuti chivomezi chija chichitike. Amosi adati, “Chauta akukhuluma ku Ziyoni, mau ake akumveka ngati bingu ku Yerusalemu. Nchifukwa chake mabusa akuuma, msipu wa pa phiri la Karimele ukufota.” Zimene akunena Chauta ndi izi: “Chifukwa anthu a ku Damasiko akunka nachimwirachimwira, sindileka kuŵalanga. Iwo ankazunza anthu a ku Giliyadi mwankhanza. Tsono Ine ndidzaponya moto pa nyumba ya Hazaele, ndipo motowo udzatentha malinga a Benihadadi. Ndidzathyola mpiringidzo woteteza mzinda wa Damasiko. Ndidzaonongeratu mfumu yolamulira ku Chigwa cha Aveni, ndiponso iye amene akugwira ndodo yaufumu ku Betedeni. Anthu a ku Siriya adzatengedwa ukapolo kupita nawo ku dziko la Kiri.” Akuterotu Chauta. Zimene akunena Chauta ndi izi: “Chifukwa anthu a ku Gaza akunka nachimwirachimwira, sindileka kuŵalanga. Iwo adatenga mtundu wathunthu wa anthu kunka nawo ku ukapolo, ndipo adaupereka ku Edomu. Tsono Ine ndidzaponya moto pa makoma ozinga Gaza, udzatentha malinga ake. Ndidzaonongeratu onse okhala ku Asidodi, kudzanso iye amene akugwira ndodo yaufumu ku Asikeloni. Ndidzakantha mzinda wa Ekeroni ndi dzanja langa, ndipo Afilisti onse otsalira adzaonongeka.” Akuterotu Ambuye Chauta. Zimene akunena Chauta ndi izi: “Chifukwa anthu a ku Tiro akunka nachimwirachimwira, sindileka kuŵalanga. Iwo adapereka mtundu wathunthu wa anthu ku Edomu, osasunga chipangano chaubale chija. Ndiye Ine ndidzaponya moto pa makoma ozinga Tiro, ndipo motowo udzatentha malinga ake.” Zimene akunena Chauta ndi izi: “Chifukwa anthu a ku Edomu akunka nachimwirachimwira, sindileka kuŵalanga. Iwo adathamangitsa abale ao lupanga lili kumanja, popanda nchifundo chomwe. Ndiponso anali ndi ukali wosatonthozeka, ndi mkwiyo wosapozeka. Ndiye Ine ndidzaponya moto pa mzinda wa Temani, ndipo motowo udzapsereza ndi malinga a ku Bozira omwe.” Zimene akunena Chauta ndi izi: “Chifukwa Aamoni akunka nachimwirachimwira, sindileka kuŵalanga. Iwo pofuna kufutuza malire ao, adatumbula akazi apakati ku Giliyadi, Ndiye Ine ndidzaponya moto pa makoma a ku Raba, ndipo motowo udzapsereza malinga ake. Padzakhala kufuula kwakukulu pa tsiku lankhondolo, kumenyana kudzakhala kwafumbi ngati mkuntho wa kamvulumvulu. Tsono mfumu yao idzatengedwa kunka ku ukapolo, iyoyo pamodzi ndi nduna zake.” Akuterotu Chauta. Zimene akunena Chauta ndi izi: “Chifukwa Amowabu akunka nachimwirachimwira, sindileka kuŵalanga. Iwo adanyoza mafupa a mfumu ya ku Edomu poŵatentha mpaka kuŵasandutsa phulusa. Nchifukwa chake Ineyo ndidzaponya moto ku Mowabu, ndipo motowo udzapsereza malinga a ku Keriyoti. Anthu a ku Mowabu adzafera pakati pa phokoso la nkhondo, asilikali akufuula ndi kuliza malipenga. Ndidzaŵaphera wolamulira wao, Ndidzaphanso nduna zake pamodzi naye.” Akuterotu Chauta. Zimene akunena Chauta ndi izi: “Chifukwa anthu a ku Yuda akunka nachimwirachimwira, sindileka kuŵalanga. Iwo anyoza malamulo a Ine Chauta, ndipo sadatsate malangizo anga. Milungu yabodza imene makolo ao ankaipembedza yaŵasokeretsa. Nchifukwa chake Ineyo ndidzaponya moto ku Yuda, ndipo motowo udzapsereza malinga a Yerusalemu.” Zimene akunena Chauta ndi izi: “Chifukwa anthu a ku Israele akunka nachimwirachimwira, sindileka kuŵalanga. Iwo amagulitsa anthu achilungamo ndi siliva, amagulitsa anthu osauka ndi nsapato. Anthu osauka iwo amaŵadyera masuku pa mutu, anthu ozunzika iwo safuna kuŵayang'ana. Bambo ndi mwana amakagona ndi mdzakazi mmodzimmodzi, mwakuti amanyoza dzina langa loyera. Anthuwo amagona pambali pa malo aliwonse opembedzerapo, pa zovala zimene adalandira kwa osauka ngati chikole. M'nyumba ya Mulungu amamweramo zakumwa za anthu amene adaŵalipitsa pa mlandu. “Komabe ndine amene ndidaononga Aamori pamene Aisraele ankafika, ngakhale iwo aja anali ataliatali ngati mikungudza, ngakhale anali amphamvu ngati mitengo ya thundu. Ndidaŵaonongeratu zipatso zao m'mwamba ndiponso mizu yao pansi. Inu Aisraele, ndine ndidakutulutsani ku dziko la Ejipito. Ndine ndidakutsogolerani m'chipululu zaka makumi anai, kuti mukalande dziko la Aamori lija. Ndipo ndine ndidasankha ena mwa ana anu kuti akhale aneneri, nkusankha ena mwa anyamata anu kuti akhale Anaziri. Kodi si choncho, inu anthu a ku Israele?” Akuterotu Chauta. “Koma Inu mudaŵamwetsa vinyo Anaziri aja, ndipo mudaŵalamula aneneriwo kuti, ‘Musalose.’ “Mverani, ndidzakukanikizani pansi kwanuko, ndipo mudzalira ngati ngolo yodzaza ndi katundu wopitirira muyeso. Waliŵiro sadzatha kuthaŵa, wanyonga sadzakhalanso ndi mphamvu. Wankhondo sadzapulumutsa moyo wake. Munthu wamauta sadzalimbika. Wothamanga sadzapulumuka, ndipo wokwera pa kavalo sadzapulumutsa moyo wake. Pa tsiku limenelo ngakhale wolimba mtima pakati pa anthu a mphamvu, adzathaŵa ali maliseche.” Akuterotu Chauta. Imvani mau amene Chauta adalankhula, mau okudzudzulani inu Aisraele, ndiye kuti banja lonse limene Iye adalitulutsa ku dziko la Ejipito. Adanena kuti, “Ine ndidasankha ndi kusamala inu nokha pakati pa mitundu yonse ya pa dziko lapansi. Tsono ndidzakulangani koposa chifukwa cha machimo anu onse.” “Kodi anthu aŵiri nkuyendera pamodzi, osapangana? Kodi mkango umabangula m'nkhalango, usanagwire nyama? Kodi msona wa mkango umakhuluma m'phanga mwake, usanagwire kanthu? Kodi mbalame nkukatera pa msampha pansi, popanda nyambo yake? Nanga msamphawo kodi nkufwamphuka pansipo, usanakole kanthu? Kodi lipenga lankhondo nkulira mu mzinda, anthu osachita mantha? Nanga tsoka likagwera mzinda, kodi si Chauta amene amachita zimenezo? Zoonadi, Ambuye Chauta sachita kanthu osadziŵitsa atumiki ao, aneneri, zimene akonzekera. Mkango ukabangula, kodi sachita mantha ndani? Ambuye Chauta akalankhula, kodi ndani sadzalalika?” “Ulengeze kwa anthu okhala m'malinga a ku Asidodi, ndiponso kwa okhala m'malinga a ku Ejipito, uŵauze kuti akasonkhane ku mapiri a ku Samariya, akaone zachipwirikiti ndi zachifwamba zimene zikuchitika pakati pa anthu ake.” “Sadziŵa kuchita zolungama amene amadzaza malinga ao ndi zinthu zozipeza mwankhondo ndi mwakuba.” Akuterotu Chauta. Nchifukwa chake Ambuye Chauta mau ao ndi aŵa: “Adani adzalizinga dzikolo, malinga ake adzaŵagwetsa, ndipo adzafunkha zonse zam'menemo.” Zimene akunena Chauta ndi izi: “Monga mbusa amangotolako miyendo iŵiri kapena nsonga ya khutu la nkhosa yake ikajiwa ndi mkango, ndimo m'mene adzapulumukire Aisraele okhala ku Samariya, ngati zidutswa chabe za bedi. “Mverani, muŵaimbe mlandu am'banja la Yakobe,” akutero Ambuye Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse. “Pa tsiku limene ndidzalange Israele chifukwa cha zolakwa zake, maguwa a ku Betele ndidzaŵagumula, ndipo nyanga za guwa zidzathyoka nkugwa pansi. Ndidzagwetseratu nyumba za nthaŵi yachisanu ndi za nthaŵi yamafundi. Nyumba zaminyanga zidzaonongeka, ndithu nyumba zazikulu zidzaphwasuka.” Akuterotu Chauta. Mverani mau aŵa akazi inu okhala ku Samariya amene mukungonenepa ngati ng'ombe za m'dera la Basani, inu amene mumavutitsa osauka ndi kuzunza osoŵa. Ntchito nkumangolamula amuna anu kuti, “Tipatseni zoziziritsa kukhosi.” Ambuye Chauta, ndi kuyera kwao kuja, alumbira kuti, “Pali Ine ndemwe, masiku a chilango chanu akudza ndithu! Nthaŵiyo anthu adzakuguguzani ndi ngoŵe. Adzakukokani ndi mbedza nonse mpaka wotsiriza. Mudzatulukira m'ming'alu ya malinga, aliyense payekhapayekha ndipo adzakutayani ku phiri la Halimoni.” Akuterotu Chauta. “Bwerani ku malo oyera ku Betele, mudzachimwireko. Bweranazoni nsembe zanu m'maŵa mulimonse, bweranazoni zopereka zanu zachikhumi pa masiku atatu aliwonse. Mupereke buledi wanu kuti muthokoze Mulungu. Munene poyera ndi kulengeza zopereka zanu zaufulu, pakuti nzimene mumakonda kuchita, inu Aisraele.” Akutero Chauta. “Ndine amene ndidakusendetsani milomo m'mizinda yanu yonse. Ndine amene ndidagwetsa njala konse kumene munkakhala. Komabe simudabwerere kwa Ine.” Akutero Chauta. “Ndinenso amene ndidamanga mvula patangotsala miyezi itatu kuti mukolole. Ndine amene ndinkagwetsa mvula pa mudzi wina, koma pa mudzi wina ai. Mvula inkagwa pa munda wina, koma munda wina nkumakhala gwa, chifukwa chosoŵa mvula. Motero midzi iŵiri kapena itatu inkapita ku mudzi umodzi kuti ikamwe madzi, koma osaŵakwanira. Komabe simudabwerere kwa Ine.” Akutero Chauta. “Ndidaumitsa mbeu zanu ndi matenda ndiponso ndi chinoni. Chidafotetsa mbeu za m'minda yanu yonse ndi yamphesa yomwe. Dzombe lidaononga mikuyu yanu ndi mitengo ya olivi, komabe simudabwerere kwa Ine.” Akutero Chauta. “Ndidakugwetserani miliri yonga ya ku Ejipito ija. Ndidaphetsa achinyamata anu ku nkhondo, ndidapereka akavalo anu kwa adani. Ndidakununkhitsani fungo la mitembo lochokera ku misasa yanu yankhondo. Komabe simudabwerere kwa Ine.” Akutero Chauta. “Ndidaononga ena mwa inu, monga momwe ndidaonongera Sodomu ndi Gomora. Otsaliranu munali ngati zikuni zofumula pa moto. Komabe simudabwerere kwa Ine.” Akutero Chauta. “Tsono inu Aisraele ndidzakuteroni. Ndipo chifukwa choti ndidzakuchitani zimenezi, inu Aisraele, konzekani kuti mukumane ndi Mulungu wanu.” Tsono tamvani, Iyeyo ndiye amene amaumba mapiri ndi kupanga mphepo, ndiye amene amaululira munthu za m'maganizo mwake, ndiye amene amasandutsa usana kuti ukhale usiku, ndiye amene amayenda pa zitunda za dziko lapansi. Dzina lake ndi Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse. Inu banja la Israele imvani mau aŵa, amene ndikukuuzani mwadandaulo: “Namwali Israele wagwa chonse osati nkudzukanso ai. Wagwa ndi kuiŵalika pa dziko lake, popanda wina womdzutsa.” Zimene akunena Ambuye Chauta ndi izi: “Mzinda umene udapita ku nkhondo ndi anthu chikwi udzatsala ndi anthu zana limodzi chabe. Ndipo umene udapita ku nkhondo ndi anthu zana limodzi, udzatsala ndi anthu khumi okha a m'banja la Israele.” Mau a Chauta ouza banja la Israele ndi aŵa: “Muchite zimene Ine ndifuna, kuti mukhalebe ndi moyo, koma musasonkhane ku Betele, ndipo musakaloŵe ku Giligala, kapena kuwolokera ku Beereseba. Ndithu a ku Giligala adzatengedwa kupita ku ukapolo, ndipo Betele adzaonongekeratu.” Muchite zimene Chauta afuna, kuti mukhalebe ndi moyo. Mukapanda kutero, adzatentha banja la Yosefe ngati moto, ndipo motowo udzapsereza a ku Betele popanda wina wouzimitsa. Tsoka kwa inu amene mumasandutsa chilungamo kuti chikhale choipa, inu amene mumanyoza zolungama. Iye uja ndiye amene adalenga nyenyezi za Akamwiniatsatana ndiponso Nsangwe, ndiye amene amasandutsa mdima kuti ukhale m'maŵa nasandutsa usana kuti ukhale usiku. Ndiye amene amaitana madzi am'nyanja ndi kuŵathira pa dziko lapansi. Dzina lake ndi Chauta. Ndiyenso amene amakantha olamulira ankhanza, ndiye amene amagumula malinga ao. Inu mumadana ndi muweruzi wodzudzula zosalungama, mumanyansidwa ndi wokamba zoona pa bwalo lamilandu. Mumapondereza anthu osauka ndi kuŵabera pa msonkho. Nchifukwa chake ngakhale mwamanga nyumba za miyala yosema, simudzakhalamo. Ngakhale mwalima minda yabwino ya mphesa, simudzamumwa vinyo wake. Ine ndikudziŵa kuchuluka kwa zolakwa zanu ndi kukula kwa machimo anu. Inu mumazunza anthu ochita chilungamo, mumalandira ziphuphu ndiponso mumapotoza milandu ya anthu osauka. Nchifukwa chake pa nthaŵi yotere munthu wanzeru salankhulapo kanthu, chifukwa ndi nthaŵi yoipa. Muike mtima pa zabwino osati pa zoipa, kuti mukhalebe ndi moyo. Apo Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, adzakhala nanu monga mwaneneramo. Muzidana ndi zoipa, muzikonda zabwino. Mukhazikitse chilungamo m'mabwalo a milandu. Mwina mwake Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, adzakukomerani mtima inu anthu otsala a m'banja la Yosefe. Nchifukwa chake zimene akunena Chauta, Ambuye, Mulungu Wamphamvuzonse, ndi izi: “M'mabwalo monse mudzakhala kulira, ndipo m'miseu monse anthu azidzangoti, ‘Mayo! Mayo!’ Ngakhale anthu wamba adzaŵaitana kuti adzalire, adzaitananso anthu odziŵa kubuma maliro kuti adzalire. M'minda yonse ya mphesa mudzakhala kulira kokhakokha, pakuti ndidzakulanganidi nonsenu.” Akuterotu Chauta. Tsoka kwa inu amene mumalilakalaka tsiku la Chauta! Kodi tsiku limenelo lidzakupinduliraninji inuyo? Kudzakhalatu mdima, osati kuŵala ai. Kudzakhala monga m'mene kumachitira munthu akamathaŵa mkango, ndipo akumana ndi chimbalangondo, kapena monga munthu woti wakaloŵa m'nyumba, atsamira chipupa ndi dzanja lake, njoka nkumuluma. Kodi suja tsiku la Chauta ndi mdima wokhawokha osati kuŵala, kodi suja lili ngati usiku wabii wopanda mpoti mbee pomwe! Chauta akuti, “Masiku anu achikondwerero ndimadana nawo ndipo ndimaŵanyoza. Misonkhano yanu yachipembedzo siindikondwetsa konse. Ngakhale mudzapereke nsembe zanu zopsereza ndiponso zaufa, Ine sindidzazivomera. Nsembe zanu zachiyanjano zophera ng'ombe zonenepa sindidzaziyang'ana nkomwe. Musandisokose nazo nyimbo zanu zachipembedzo, sindingathe kupirira kulira kwa azeze anu. Koma kuweruza kwanu kwangwiro kuziyenda kosalekeza ngati madzi, kulungama kwanu kukhale ngati mtsinje wosaphwa. “Kodi inu anthu a ku Israele, zaka makumi anai zimene mudakhala m'chipululu, mudanditsirirako nsembe ndi kundipatsa mitulo? Ndipotu muzidzanyamula Sakuti, mfumu yanu, ndi nyenyezi ija Kaiwani, mulungu wanu, mafano amene mudadzipangira. Pakuti ndidzakupititsani ku ukapolo, kutali kupitirira mzinda wa Damasiko.” Akutero Chauta, amene dzina lake ndi Mulungu Wamphamvuzonse. Tsoka kwa inu amene mumakhala mosatekeseka ku Ziyoni, ndiponso kwa inu amene mumakhala mosavutika ku Samariya. Tsoka kwa inu anthu otchuka pakati pa Aisraele, inu amene anthu onse amafika kwanu. Pitani ku mzinda wa Kaline mukaone. Mupitenso ku Hamati mzinda wotchuka uja, tsono mutsikire ku Gati kwa Afilisti. Kodi Aisraelenu mukupambana anthu a mafumu ameneŵa? Kodi kapena dziko lao nlalikulu kupambana lanu? Inu simulabadako zoti kudzafika tsiku lachilango, zochita zanu zimafulumizitsa nthaŵi yachiwawayo. Tsoka kwa inu amene mumagona pa mabedi oŵakongoletsa ndi minyanga yanjovu, inu amene mumangoti lamzi pa mipando yanu, nkumachita phwando la nyama ya anaankhosa osakhwima ndi ya anaang'ombe onenepa. Ntchito nkumangoimba azeze ngati Davide, ndi kumangopeka nyimbo zoimbira pa zing'wenyeng'wenye. Tsoka kwa inu amene mumamwera vinyo m'zipanda zodzaza, inu amene mumadzola mafuta abwino kwambiri, koma simumva chisoni ndi kuwonongeka kwa dziko la Yosefe. Nchifukwa chake mudzatsogola ndinu kupita ku ukapolo, ndipo maphwando ndi zikondwerero zidzakutherani. Ambuye Chauta alumbira m'dzina lao kuti, “Ndikunyansidwa ndi zimene ana a Yakobe akunyadira, ndikudana nazo nyumba zao zazikulu. Ndithu ndidzapereka kwa adani ao likulu lao ndi zonse zam'menemo.” Anthu khumi akadzakhala akubisala m'nyumba imodzi, nawonso adzafabe. Mbale wake wa wina mwa akufawo, woyenera kusamala za maliro, adzafika kudzatulutsa mtembo m'nyumbamo. Tsono adzafunsa wina amene watsalakobe m'nyumbamo kuti, “Kodi uli ndi winanso wamoyo m'menemo?” Iyeyo adzayankha kuti, “Ai mulibiretu.” Ndipo mbaleyo adzati, “Khala chete, iwe! Tisayerekeze kutchula dzina la Chauta.” Zoonadi, Chauta akadzangolamula, nyumba zikuluzikulu zidzagamukagamuka, ndipo nyumba zing'onozing'ono ndiye zidzangosanduka zibuma zokhazokha. Kodi pa thanthwe akavalo nkuthamangapo? Kodi panyanja wina nkulimapo ndi ng'ombe? Komabe chilungamo mwachisandutsa chivumulo, ndipo zaungwiro mwazisandutsa zoŵaŵa. Mukunyadira kuti mudagonjetsa mzinda wa Lodebara, mukunena kuti, “Kodi suja tidapambana mzinda wa Karinaimu ndi mphamvu zathu zokha?” Koma Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse akuti, “Ndidzakuputirani anthu a mtundu wina kuti adzakuthireni nkhondo, inu Aisraele. Adzakuzunzani kuyambira ku Mpata wa Hamati kumpoto mpaka ku mfuleni wa Araba kumwera.” Izi ndizo zimene Ambuye Chauta adandiwonetsa m'masomphenya: Chauta ankapanga dzombe pa nthaŵi yoti mfumu inali itamweta kale udzu, ndipo udzuwo unkaphukanso kachiŵiri. Pamene ndidaona kuti dzombelo ladya zomera zonse zam'dzikomo, ndidati, “Inu Ambuye Chauta, ndapota nanu, khululukani. Kodi anthu a Yakobeŵa angalimbike bwanji? Iwoŵa ndi ofooka kwambiri.” Apo Chauta adakhululuka, ndipo adati, “Zimenezi sizidzachitika konse.” Zina ndi izi zimene Ambuye Chauta adandiwonetsa m'masomphenya: Ambuye Chauta ankaitana malaŵi a moto kuti alange anthu. Motowo udapsereza phompho lalikulu, nuyamba kuwononga minda yonse ya pa dziko lapansi. Tsono ine ndidati, “Inu Ambuye Chauta, ndapota nanu, basi lekani. Kodi anthu a Yakobeŵa angalimbike bwanji? Iwoŵa ndi ofooka kwambiri.” Apo Chauta adakhululuka, ndipo adati, “Zimenezinso sizidzachitika konse.” Zina ndi izi zimene Chauta adandiwonetsa m'masomphenya: Ndidaona Iye ataima pamwamba pa khoma lomangamanga, m'manja mwake ali ndi chingwe choongolera khoma. Tsono Chautayo adandifunsa kuti, “Kodi iwe Amosi, nchiyani ukuwonachi?” Ine ndidayankha kuti, “Chingwe choongolera khoma.” Apo Chauta adati, “Ndikuika chingwe chimenechi pakati pa anthu anga Aisraele kuti kuwoneke kukhota kwao, choncho sindidzaŵalekereranso ai. Akachisi a ana a Isaki adzasanduka bwinja, malo achipembedzo a Aisraele adzaonongedwa. Ndipo ndidzagwetsa banja la mfumu Yerobowamu pa nkhondo.” Ku Betele kunali wansembe wina dzina lake Amaziya. Iyeyo adatumiza mthenga kwa Yerobowamu, mfumu ya ku Israele kuti, “Amosi akukuutsirani chiwembu pakati pa anthu a ku Israele. Anthu sangathe kuvomera zonse zimene iye akunenazo. “Amosiyo akunena kuti, ‘Yerobowamu adzafa pa nkhondo, ndipo Aisraele adzatengedwa kunka ku ukapolo, kutali ndi dziko lao.’ ” Tsono Amaziya adauza Amosi kuti, “Mlosi iwe, choka kuno! Thaŵira ku dziko la Yuda! Uzikalosa kumeneko, ndipo anthu akumeneko azikakudyetsa. Koma usakalosenso ku Betele poti kumeneko ndi malo opatulika a mfumu, ndiponso ndi Nyumba ya Mulungu ya m'dziko lino.” Amosi adayankha Amaziya kuti, “Ine sindine mneneri konse, kapenanso wa m'gulu la aneneri. Inetu ndine woŵeta nkhosa, ndiponso wolima nkhuyu. Chauta adachita kukanditenga, kundileketsa ntchito yoŵeta nkhosa, nandiwuza kuti, ‘Pita, ukalalikire anthu anga, Aisraele.’ “Nchifukwa chake tsono imva mau amene Chauta akunena. Iweyo ukundiwuza kuti ndisalose zotsutsa Israele, ndisalalike zotsutsa banja la Isaki. Tsono zimene akunena Chauta ndi izi: ‘Mkazi wako adzasanduka mkazi wadama mumzindamu. Ndipo ana ako aamuna ndi aakazi adzaphedwa pa nkhondo. Dziko lako adzaligaŵagaŵa kugaŵira anthu ena. Iweyo ukafera ku dziko lachikunja. Ndipo Aisraele adzatengedwa kunka ku ukapolo kutali ndi dziko lao.’ ” Zinanso zimene Ambuye Chauta adandiwonetsa m'masomphenya ndi izi: Panali dengu la zipatso zakupsa. Chauta adandifunsa kuti, “Kodi iwe Amosi, nchiyani ukuwonachi?” Ine ndidayankha kuti, “Dengu la zipatso zakupsa.” Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Nthaŵi ya chimalizo yaŵakwanira anthu anga Aisraele, sindidzaŵakhululukiranso. Nyimbo za m'Nyumba ya Mulungu zidzasanduka kulira pa tsiku limenelo. Mitembo ya anthu idzachuluka, ndipo adzaiponya ponseponse. Kudzangoti zii!” Akuterotu Ambuye Chauta. Amosi adati, “Imvani izi, inu amene mumapondereza osoŵa, amene mufuna kuwononga anthu osauka am'dzikomu. Inu mumadzifunsa kuti, ‘Kodi chikondwerero cha kukhala kwa mwezi chidzatha liti, kuti tigulitse dzinthu? Kodi tsiku lopumula la Sabata litha liti kuti tigulitsenso tirigu, kutinso tipeze mpata wochepetsera miyeso ndi kukweza mitengo, ndiponso kuti tichenjeretse anthu ndi masikelo onama, kuti osauka tiŵagule ndi siliva, amphaŵi tiŵagule ndi nkhwaŵiro, kutinso tigulitse ndi mungu womwe wa tirigu?’ ” Chauta, Mulungu amene ana a Yakobe amamnyadira walumbira kuti, “Ndithudi, sindidzaiŵala zochita zao zonse. Chifukwa cha zonsezi dziko lapansi lidzagwedezeka, ndipo onse okhala m'menemo adzamva chisoni! Dziko lonse lapansi lidzagwedezeka ngati Nailo, lidzafufuma ndi kuteranso ngati mtsinje wa Nailo wa ku Ejipito.” Ambuye Chauta akunena kuti, “Pa tsiku limenelo ndidzadetsa dzuŵa masana, ndidzagwetsa mdima pa dziko lapansi dzuŵa lili nye. Zikondwerero zanu ndidzazisandutsa kulira, nyimbo zanu ndidzazisandutsa zamaliro. Ndidzakuvekani chiguduli nonsenu pathupi panu, ndipo mitu yanu yonse idzachita dazi. Mudzakhala ngati anakubala olira mwana wao mmodzi yekha. Tsiku limenelo lidzakhaladi loŵaŵa mpaka kutha kwake.” Ambuye Chauta akunena kuti, “Nthaŵi ikubwera pamene ndidzagwetsa njala m'dzikomo. Siidzakhala njala ya buledi, kapena ludzu la madzi ai, koma njala yosoŵa mau a Chauta. Anthu azidzangoyenda uku ndi uku kuchoka ku nyanja ina kunka ku nyanja inanso, azidzangoti piringupiringu kuchoka chakumpoto kunka chakuvuma. Azidzafunafuna mau a Chauta, koma osaŵapeza. “Pa tsiku limenelo ngakhale anamwali abiriŵiri ndi anyamata asee adzakomoka ndi ludzu. Onse amene amalumbira m'dzina la Asima, mulungu wa Samariya, nkumanena kuti, ‘Pali mulungu wa ku Dani!’ Kapena kuti, ‘Pali njira yopatulika ya ku Beereseba!’ Onsewo adzagwa osadzukanso.” Tsono ndidaona Chauta ataima pambali pa guwa. Adati, “Gwetsani makapotolosi a Nyumba ya Mulungu, kuti maziko ake agwedezeke. Muŵagwetsere pamitu pa anthu. Onse otsalira Ine ndidzaŵapha pa nkhondo. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzathaŵe. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzapulumukepo. “Ngakhale akakumbe pansi mpaka ku malo a anthu akufa, dzanja langa lidzaŵadukhululako kumeneko. Ngakhale akakwere mpaka kumwamba, ndidzaŵatsakamutsako. Ngakhale akabisale pamwamba pa phiri la Karimele, ndidzaŵaunguza nkuŵagwira. Ngakhale akabisale pansi pa nyanja yaikulu, ndidzalamula chilombo cham'nyanjamo kuti chiŵalume. Ngakhale adani ao aŵakusire ku ukapolo, komweko ndidzalamula kuti aphedwe pa nkhondo. Ndidzaŵayang'anitsitsa kuti ziŵagwere zoipa osati zabwino.” Ambuye Chauta Wamphamvuzonse, akakhudza dziko, limanyenyeka, ndipo zonse zokhala m'menemo zimalira. Apo dziko lonse limafufuma ngati mtsinje wa Nailo ndipo limateranso ngati mtsinje wa Nailo wa ku Ejipito. Ndiwo amene amamanga malo ao okhalamo kumwamba, naika thambo ngati denga la dziko lapansi, amaitana madzi akunyanja naŵakhuthulira pa dziko lapansi. Iwowo dzina lao ndi Chauta. “Kwa Ine, Aisraelenu muli ngati Aetiopiya.” Akuterotu Chauta. “Kodi sindine uja ndidatulutsa Aisraele ku Ejipito? Kodi sindine uja ndidatulutsa Afilisti ku Kafitori ndi Asiriya ku Kiri? Ine, Ambuye Chauta, maso anga ali pa dziko lochimwalo, ndipo ndidzalifafaniza pa dziko lapansi. Komabe banja la Yakobe lokha sindidzaliwononga kotheratu.” Akuterotu Chauta. “Ai, ndidzalamula, ndipo ndidzagwedeza Aisraele uku ndi uku pakati pa mitundu yonse ya anthu monga momwe amagwedezera sefa uku ndi uku, popanda kamwala nkamodzi komwe kogwa pansi. Adzafera pa nkhondo anthu anga onse ochimwa, iwo amene amati, ‘Chilango sichidzatifika, kapena kutipambana.’ ” Chauta akuti, “Nthaŵi imeneyo ndidzakwezanso ufumu wa Davide umene udagwa ngati nyumba. Ndidzakonzanso makoma ake ogumuka ndi kumanganso mabwinja ake. Ndidzaubwezeranso mwake mwakale. Nthaŵi imeneyo Aisraele otsala adzagonjetsa zimene zatsala za ku Edomu, pamodzi ndi maiko onse amene amadziŵika ndi dzina langa.” Akuterotu Chauta, amene adzachitedi zimene wanenazi. Chauta akunena kuti, “Nthaŵi ikubwera pamene mlimi adzabzola wokolola, ndipo woponda mphesa adzabzola wobzala mbeu. M'mapiri mudzatuluka vinyo wokoma, azidzachita kuyenderera pa zitunda zonse. “Ndidzaŵabwezeranso pabwino anthu anga Aisraele. Adzamanganso mizinda yamabwinja ndi kumakhalamo. Adzalima minda ya mphesa ndipo adzamwa vinyo wake. Adzalima minda ndipo adzadya zipatso zake. Ndidzaŵakhazikanso m'dziko mwao, ndipo palibe amene adzaŵachotsemo m'dziko limene ndidzaŵapatsalo.” Akuterotu Chauta, Mulungu wanu. Izi ndi zimene Obadiya adaona m'masomphenya. Naŵa mau a Ambuye Chauta onena za Aedomu. Chauta adatuma wamthenga wake kwa anthu a mitundu yonse, ndipo tidamva mau ake, adati, “Konzekani, tiyeni tikamenyane nkhondo ndi Aedomu.” Chauta akuuza Aedomu kuti, “Ndithu ndidzakutsitsani kotheratu, anthu a mitundu yonse adzakunyozani kwambiri. Mwanyengedwa ndi mtima wanu wonyada. Likulu lanu lili pakati pa matanthwe, mumakhala pa mapiri aatali. Mumanena kuti, ‘Ndani angatitsitse pansi?’ Komatu ngakhale muuluke pamwamba ngati chiwombankhanga, ngakhale mumange chisa chanu pakati pa nyenyezi, ndidzakutsitsanibe pansi.” Akutero Chauta. “Akuba akabwera usiku, amangotengako zimene akufuna. Okolola akamathyola zipatso, amasiyako zina. Koma inuyo adani anu akupululani kotheratu. Onani m'mene alisakazira dziko la Esau, ndi m'mene achifunkhira chuma chake chonse. Ogwirizana nanu akunyengani, akupirikitsani m'dziko mwanu. Okuthandizani pa nkhondo akugonjetsani. Abwenzi anu apamtima akutcherani msampha, mwathedwa nzeru tsopano.” Chauta akuti, “Nthaŵi imeneyo ndidzaononga anzeru onse a ku Edomu, ndidzathetsa kuchenjera konse kwa zidzukulu za Esau. Ngwazi za ku Temani zidzachita mantha, ankhondo onse adzaphedwa ku mapiri a Esau. “Aedomu inu, chifukwa cha zankhanza zimene mudachita abale anu, zidzukulu za Yakobe, adzakuchititsani manyazi ndi kukuwonongani mpaka muyaya. Munkangoonerera pamene adani ankaŵalanda chuma chao, munkachita ngati kuvomerezana nawo, amene ankaloŵa pa zipata za Yerusalemu, namagaŵana chumacho. Inu simukadayenera kuŵanyodola abale anu Ayuda chifukwa cha tsoka lao. Simukadayenera kukondwerera kuwonongeka kwao. Simukadayenera kuŵaseka pamene iwo anali m'mavuto. Pa tsiku lao la tsoka simukadayenera kuloŵa mu mzinda wa anthu anga. Pa tsiku lao la tsoka simukadayenera kuŵanyodola. Pa tsiku lao la tsoka simukadayenera kulanda chuma chao. Simukadayenera kudikira pa mphambano za miseu kuti mugwire anthu othaŵa. Pa tsiku lao la tsoka simukadayenera kupereka anthu ao otsala kwa adani. “Posachedwapa lifika tsiku la Chauta pamene Iye adzaweruza mitundu yonse ya anthu. Aedomu inu, adzakuchitani zomwe mudaŵachita ena. Zimene mudachitazo zidzakubwererani. Anthu anga adamwa chikho cha zoŵaŵa pa phiri langa loyera, koma mitundu ina ya anthu idzamwa chikho cha zoŵaŵa kopitirira. Idzachita kugugudiza chikhocho kenaka nkuzimirira pomwepo. “Koma pa phiri la Ziyoni padzakhala ena opulumuka, ndipo phirilo lidzakhala loyera. Pamenepo fuko la Yakobe lidzalandira choloŵa chakechake. Fuko la Yakobe lidzakhala ngati moto, fuko la Yosefe lidzakhala ngati malaŵi a moto, fuko la Esau lidzakhala ngati ziputu. Adzaŵatentha ndi kuŵapsereza, ndipo sipadzapulumuka munthu aliyense.” Akutero Chauta. Ayuda akumwera adzalandira phiri la Esau, akuzambwe adzalandira dziko la Afilisti. Akumpoto adzalandira dziko la Efuremu ndi likulu lake Samariya, ndipo Abenjamini adzalandira dziko lakuvuma la Giliyadi. Aisraele amene anali ku ukapolo adzalandira dziko la Kanani mpaka kumpoto ku Zarefati. A ku Yerusalemu amene anali ku ukapolo ku Sefaradi adzalandira mizinda yakumwera ku Negebu. Ngwazi zochokera ku Yerusalemu zidzagonjetsa ndi kumalamulira dziko la Edomu ndipo ufumu wonse udzakhala wa Chauta. Tsiku lina Chauta adapatsa Yona, mwana wa Amitai, uthenga uwu wakuti, “Nyamuka, upite ku Ninive, mzinda waukulu uja. Ukaŵadzudzule momveka ndithu anthu chifukwa ndaona kuipa kwao.” Koma Yona pofuna kuthaŵa Chauta, adanyamuka nkumapita ku Tarisisi. Adapita ku mzinda wa Yopa, kumene adapeza chombo chopita ku Tarisisi. Adagula tikiti naloŵa m'chombomo, kuti apite nao ku Tarisisi, kuti choncho athaŵe Chauta. Koma Chauta adautsa namondwe, ndipo nyanja idayamba kuŵinduka kwambiri ndi namondweyo, kotero kuti chombo chinali pafupi kuwonongeka. Amalinyero adachita mantha, aliyense nkumalirira mulungu wake. Adayamba kuponya katundu m'nyanja kuti chombo chipepuke. M'menemo nkuti Yona atatsikira m'katikati mwa chombo, ali m'tulo tofa nato. Tsono kaputeni wa chombo adafika kwa Yona uja namufunsa kuti, “Kodi iwe, nchiyani chimenechi? Monga iwe nkumagona eti? Dzuka, utame kwa Mulungu wako mopemba, mwina nkuwona watithandiza kuti tisamire.” Amalinyerowo adayamba kuuzana kuti, “Tiyeni tichite maere kuti tipeze amene wabweretsa masoka ameneŵa.” Choncho adachitadi maerewo, ndipo adagwera Yona. Tsono adamufunsa kuti, “Tatiwuza, masoka ameneŵa atigwera chifukwa cha yani? Umagwira ntchito yanji? Ukuchokera kuti? Kwanu nkuti? Ndiwe mtundu wanji?” Iye adayankha kuti, “Ndine Muhebri, ndimapembedza Chauta, Mulungu wa Kumwamba, amene adalenga nyanjayi ndi mtundawu.” Pamenepo amalinyero aja adachita mantha kwambiri, namufunsa kuti, “Kodi wachita chiyani?” Kudziŵa adaadziŵa kuti Yona ankathaŵa Chauta, poti anali ataŵauza kale. Tsono adamufunsa kuti, “Kodi tikuchite chiyani kuti nyanjayi ikhale bata?” M'menemo nkuti namondwe uja akukulirakulira. Yonayo adaŵauza kuti, “Chabwino, ingondiponyani m'nyanjamu, mukatero nyanjayi ikhala bata. Ndikudziŵa kuti wolakwa ndine, nkuwona namondweyu akukuvutani chotere.” Amalinyero adayesetsa kupalasa kwambiri kuti abwerere ku mtunda, koma adalephera ndithu, poti mafunde ankakwererakwerera. Tsono adatama Chauta mopemba kuti, “Inu Chauta, takupembani musalole kuti ifeyo tife chifukwa cha moyo wa munthu uyu. Musatizenge mlandu chifukwa cha kupha munthu wosalakwa. Zonsezi zachitika chifukwa cha kufuna kwanu Inu Chauta.” Atatero adagwira Yona namponya m'nyanja. Pompo nyanjayo idakhala bata. Amalinyerowo adachita mantha aakulu ndi Chauta. Tsono adapereka nsembe, nalonjeza kuti adzatumikira Chauta. Chauta adatuma chinsomba chachikulu kuti chimeze Yona. Motero Yonayo adakhala m'mimba mwa chinsombacho masiku atatu, usana ndi usiku. Tsono Yona ali m'mimba mwa chinsomba chija, adayamba kutama Chauta mopemba. Adati, “Inu Chauta, pamene ndinali m'mavuto ndidakuitanani, ndipo mudandiyankha. Pamene ndinali m'dziko la akufa ndidalira kwa Inu kuti mundithandize, ndipo mudamva pempho langa. Mudandiponya m'nyanja yozama, m'kati mwenimweni mwa njanja, ndipo mweza wam'nyanjamo udandizungulira. Pamene ndidati, ‘Mwanditaya kutali ndi Inu. Kodi ndidzaiyang'ananso bwanji Nyumba yanu yoyera?’ Madzi adandiyesa m'khosi, nyanja yozama idandizungulira. Udzu wakayandeyande udandikwidzinga m'mutu. Ndidatsikira kunsi ndithu, m'tsinde mwa mapiri, kudziko kumene mipiringidzo idanditsekera mpaka muyaya. Koma Inu Chauta, Mulungu wanga, mudanditulutsa kumandako ndili moyo. Poona kuti ine nkufatu kuno, ndidakumbukira Inu Chauta, pemphero langa lidakufikani m'Nyumba yanu yoyera. Anthu opembedza milungu yachabe amataya kukhulupirika kwao. Koma ine ndidzapereka nsembe kwa Inu ndi mau okuthokozani. Zimene ndidalonjeza ndidzazichita ndithu. Chipulumutso nchochokera kwa Inu Chauta.” Apo Chauta adalamula chinsomba chija kuti chisanzire Yona ku mtunda. Chauta adalankhula ndi Yona kachiŵiri, namuuza kuti, “Nyamuka, pita ku Ninive, mzinda waukulu uja, ukaulalikire uthenga umene ndikukuuza.” Yona adanyamuka, napita ku Niniveko, potsata mau a Chauta. Mzindawo unali waukulu kwambiri, wofunika masiku atatu kuudutsa. Yona adaloŵa mumzindamo, nayenda ulendo wa tsiku limodzi. Adayamba kulalika kuti, “Pakapita masiku makumi anai, Ninive aonongeka!” Anthu a ku Ninive adakhulupirira Mulungu. Adalengeza kuti aliyense, wamkulu ndi wamng'ono yemwe, asale zakudya, ndipo avale chiguduli. Mfumu ya ku Ninive itamva zimenezo, idatsika pa mpando wake waufumu, nivula mkanjo wake. Idavala chiguduli, nikakhala nao pa dzala. Tsono mfumuyo idalengeza ku Ninive, kuti, “Nali lamulo lochokera kwa mfumu ndi akalonga ake: ‘Munthu aliyense asadye kanthu, ndiponso ziŵeto zonse zikuluzikulu ndi zing'onozing'ono zomwe zisadye kanthu. Zisadyetu kanthu, nkumwa madzi komwe zisamwe. Anthu avale ziguduli, nyamanso aziveke ziguduli. Anthuwo azifuula kwa Mulungu ndi mphamvu zao zonse. Ndithu aliyense asiye makhalidwe ake oipa ndi ntchito zake zankhanza. Nkudziŵanji, mwina Mulungu nkutikhululukira, naleka kutikwiyira, ifeyo osaonongeka.’ ” Mulungu adaona zimene anthuwo adachita, ndi m'mene adasiyira makhalidwe ao oipa. Choncho adakhululuka, osaŵapatsa chilango chimene adaati adzaŵapatsa. Chifukwa cha zimenezi Yona adakhumudwa kwambiri, nakwiya. Tsono adapemphera kwa Chauta kuti, “Inu Chauta, nzimenezitu zimene ndinkaopa ndili kwathu. Nchifukwa chake ndidaayesetsa kuthaŵira ku Tarisisi. Ndidaadziŵa kuti Inu ndinu Mulungu wokoma mtima ndi wachifundo, woleza mtima ndi wa chikondi chosasinthika, ndiponso wokhululukira machimo nthaŵi zonse. Ndiye tsono Inu Chauta, ndapota nanu, ingondiphani basi. Nkhwabwino kuti ndife kupambana kukhala moyo.” Chauta adamufunsa kuti, “Kodi iwe wachita bwino pokwiya chotere?” Yona adatuluka mumzindamo nakakhala pansi chakuvuma kwake. Kumeneko adadzimangira chithando nakhala m'menemo mu mthunzi, kudikira kuti aone zimene zichitike mumzindamo. Tsono Chauta Mulungu adameretsa msatsi kuti uchitire Yona mthunzi ndi kumchotsa mavuto ake. Yona adakondwa kwambiri chifukwa cha msatsiwo. Koma m'maŵa mwake mbandakucha, Mulungu adatuma mphanzi kuti ikadye msatsiwo, ndipo udafota. Pamene dzuŵa linkatuluka, Chauta adautsira Yona mphepo yotentha kuti iwombe kuchokera kuvuma. Dzuŵa lidamtentha pa mutu Yona, mpaka kulenguka nalo. Tsono adapempha kuti afe, adati, “Nkwabwino kuti ndife kupambana kukhala moyo.” Koma Mulungu adamufunsa kuti, “Kodi wachita bwino pokwiya chifukwa cha msatsiwu?” Iye adati, “Inde ndachita bwino kukwiya. Kukwiya kwake nkofa nako.” Chauta adati, “Iwe ukumvera chisoni msatsi umene sudaugwirire ntchito, sindiwe udaubzala ndi kuukuza. Udamera pa usiku umodzi, nufanso pa usiku umodzi. Nanga Ine, kodi sindiyenera kuumvera chisoni mzinda waukulu wa Ninive? M'mene mujatu muli anthu opitirira zikwi 120, amene sadziŵa kusiyanitsa kuti zabwino nziti, zoipa nziti, mulinso ziŵeto zochuluka.” Pa nthaŵi ya ufumu wa Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a ku Yuda, Chauta adampatsa mthenga Mika wa ku Moreseti. Nazi zimene iyeyu adaona m'masomphenya zokhudza Samariya ndi Yerusalemu. Imvani nonsenu anthu a mitundu yonse. Tchera khutu iwe dziko lapansi ndi zonse zokhala m'menemo. Ambuye Chauta akuimbani mlandu, akulankhulira ku Nyumba yao yoyera. Taonani, Chauta akubwera kuchokera ku malo ake. Akutsika pansi ndipo akuyenda pa nsonga za mapiri. Mapiriwo akusungunuka ngati phula pa moto. Akuyenderera m'zigwa ngati madzi ochokera m'phiri. Zonsezi zikuchitika chifukwa cha zoipa za zidzukulu za Yakobe, chifukwa cha machimo a banja la Israele. Ndani adachimwitsa Aisraele? Si a ku Samariya kodi? Ndani adalakwitsa Ayuda? Si a ku Yerusalemu kodi? Tsono Chauta akuti, “Samariyayo ndidzamsandutsa bwinja, malo olimamo munda wamphesa. Miyala yake ndidzaitaya ku zigwa, ndipo maziko ake ndidzaŵafukula. Mafano ake onse ndidzaŵaphwanyaphwanya, ndipo mitulo yake yonse idzatenthedwa m'moto. Zithunzi zonse za milungu yake ndidzaziwononga. Mphatso zake adazilandira kuchokera ku malipiro a akazi adama, choncho enanso adzazigwiritsa ntchito ngati malipiro a akazi adama.” Tsono Mika adati, “Nchifukwa chake ndidzalira komvetsa chisoni. Ndidzayenda maliseche, ndidzakuwa ngati nkhandwe ndi kulira ngati nthiŵatiŵa. Samariya, zilonda za uchimo wake sizingathe kupola, zafika mpaka ku Yuda. Chiwonongeko chili pafupi ndi mzinda wa anthu anga, chafika mpaka ku Yerusalemu kwenikweni.” Musaŵauze zimenezi a ku Gati, musalire konse. Muvimvinizike m'fumbi ku Beteleafura, kuwonetsa chisoni. Inu anthu a ku Safiri mudzapita ku ukapolo muli maliseche ndi amanyazi. Anthu a ku Zanani satuluka mu mzinda wao. Mukamva anthu a ku Betezele akulira, mudzadziŵa kuti sangathe kukuthandizani. Anthu a ku Maroti ali ndi nkhaŵa poyembekeza thandizo, chifukwa Chauta wadzetsa chiwonongeko pafupi ndi Yerusalemu. Mangani akavalo ku magaleta, inu anthu a ku Lakisi. Mudatsanzira machimo a Israele, potero mudachimwitsa anthu a ku Ziyoni. Tsono a ku Moreseti-Gati mutsazikane nawo. Anthu a ku Akizibu adzanamiza mafumu a ku Israele. Inunso anthu a ku Maresa, ndidzakutumirani adani kuti akugonjetseni. Akuluakulu a ku Israele adzabisala m'thanthwe la Adulamu. Inu a ku Yuda, metani mpala, kuwonetsa kuti mukulira ana anu amene munkaŵakonda. Mukhale ndi dazi la dembo poti anawo adakusiyani, adatengedwa ku ukapolo. Tsoka kwa anthu amene amakonzekera chiwembu, amene usiku wonse amalingalira ntchito zoipa. Akadzuka m'maŵa amakazichitadi, pakuti mphamvu zake ali nazo. Akasirira minda, amailanda. Akakhumbira nyumba, amazilanda. Amavutitsa munthu ndi banja lake, naŵatengera zonse zimene ali nazo. Nchifukwa chake zimene akunena Chauta ndi izi: “Imvani, ndidzakufitsirani tsoka chifukwa cha zoipa zonsezi. Ndidzakuvekani goli m'khosi mwanu, limene simungathe kulivula. Apo simudzayendanso monyada, chifukwa nthaŵi imeneyo idzakhala yoipa. Tsiku limenelo anthu adzakupekerani nthano yokunyodolani, adzakuimbani nyimbo yamaliro, adzati, ‘Taonongeka kotheratu. Dziko limene Chauta adatigaŵira, bwanji afuna kutilanda! Minda yathu aigaŵira amene atigwira ukapolo.’ ” Tsono pa nthaŵi imene Chauta adzabwezeranso dziko kwa anthu ake, inuyo simudzalandirako gawo lililonse. Anthu amandiwuza kuti, “Musatilalikire, munthu asalalike zimenezi. Manyazi sadzatigwera ai. Monga zoterezi nzoyenera kuzinena, inu a banja la Yakobe? Kodi kuleza mtima kwa Chauta kwatheratu? Kodi zimenezi nzimene adachita? Kodi mau ake sadzetsa zabwino kwa munthu woyenda molungama?” Chauta akuti, “Koma inu mumaukira anthu anga ngati mdani. Mumaŵavula mkanjo anthu amtendere, amene amangoyenda ndi mtima wokhazikika, osaganizako za nkhondo. Akazi a anthu anga mumaŵatulutsa m'nyumba zao zokoma. Ndipo ana ao mumaŵalanda madalitso anga kosalekeza. Nyamukani, chokani, ano simalo opumulirapo. Zonyansa zanu zaŵaipitsa, zadzetsapo chiwonongeko choopsa. Munthu wina atamapita uku ndi uku akulalika zabodza kuti, ‘Ndithudi mudzakhala ndi vinyo ndi zakumwa zamphamvu zambiri,’ mlaliki wotere ndi amene anthu aŵa angamkonde. “Koma inu banja lonse la Yakobe, ndidzakusonkhanitsani. Onse otsala a ku Israele ndidzaŵasonkhanitsa pamodzi ngati nkhosa m'khola, ngati gulu la zoŵeta pa busa lake. Malowo adzakhala thithithi ndi chinamtindi cha anthu.” Woŵapulumutsa adzaŵatsogolera, ndipo onse adzathyola pa chipata nathaŵa. Idzayambira ndi mfumu yao kudutsa, Chauta adzakhala patsogolo pao. Ine ndidati, “Imvani inu akuluakulu a Yakobe, olamulira a banja la Israele! Kodi oyenera kudziŵa chilungamo sindinu? Mumadana ndi zabwino, mumakonda zoipa. Anthu anga mumaŵasenda amoyo, ndi kukangadzula mnofu wao. Mumandidyera anthu anga, mumachita ngati kumaŵasenda, kuphwanya mafupa ao, ndi kumaŵachekera mumphika ngati nyama. “Nthaŵi ikubwera pamene mudzalira kwa Chauta, koma sadzakuyankhani. Nthaŵi imeneyo adzakufulatirani chifukwa ntchito zanu nzoipa.” Zimene akunena Chauta ndi izi: “Pali aneneri amene amasokeza anthu anga: amamlosera za mtendere amene amaŵadyetsa, koma amamlosera nkhondo amene alibe choŵapatsa.” Ndiye Chauta akuti, “Nchifukwa chake simudzaonanso zinthu m'masomphenya, simudzalosanso konse. Inu aneneri, kwakuderani, mdima wakugwerani.” Alauli adzaŵanyazitsa, oombeza maula adzaŵachititsa manyazi. Onse adzangoti pakamwa gwirire, chifukwa Mulungu sakuŵayankha. Koma ine Chauta wandidzaza ndi mphamvu, wandidzaza ndi mzimu wake. Wandidzaza ndi kulungama ndi kulimba mtima, kuti ndidzudzule a banja la Yakobe chifukwa cha zolakwa zao, kuti ndiwonetse Aisraele zoipa zao. Imvani izi inu atsogoleri a banja la Yakobe, inu olamulira a banja la Israele. Inu mumadana ndi chilungamo, mumakhotetsa zinthu zokhoza. Mumamanga Ziyoni ndi chuma chochipata pakupha anthu, Yerusalemu mumammanga ndi kuipa kwanu. Atsogoleri ake saweruza popanda chiphuphu, ansembe ake saphunzitsa popanda malipiro, aneneri ake salosa popanda ndalama. Komabe amagonera pa Chauta ndi kunena kuti, “Kodi suja Chauta ali pakati pathu? Tsoka silingatigwere ai.” Tsono chifukwa cha inu Ziyoni adzatipulidwa ngati munda, Yerusalemu adzasanduka bwinja, ndipo phiri la Nyumba ya Mulungu lidzasanduka nkhalango. Pa masiku akudzaŵa, phiri la Nyumba ya Chauta adzalisandutsa lalitali koposa mapiri ena onse, lidzangoti joo pamwamba pa magomo onse. Mitundu yonse ya anthu idzathamangira ku phiri limenelo. Anthu a mitundu yambiri adzabwera, ndipo adzanena kuti, “Tiyeni tikwere ku phiri la Chauta, ku Nyumba ya Mulungu wa Yakobe, ndipo adzatiphunzitsa njira zake, ndipo tiziyenda m'njira zakezo.” Pakutitu nku Ziyoni kumene kudzafumira malangizo akewo, nku Yerusalemu kumene kudzachokera mau a Chauta. Iyeyo adzaweruza pakati pa mitundu yambiri ya anthu, adzathetsa kusamvana pakati pa mafuko amphamvu, ngakhale akutali omwe. Anthuwo adzasula malupanga ao kuti akhale makasu, ndiponso mikondo yao kuti ikhale mapwitika. Mitundu ya anthu sidzasamulirananso malupanga, sidzaphunziranso zomenyana nkhondo. Koma munthu aliyense azidzangodzikhalira mwamtendere patsinde pa mtengo wake wamphesa, ndi patsinde pa mkuyu wake. Palibe amene adzaŵachititsa mantha, pakuti mwiniwake, Chauta Wamphamvuzonse, wanena zimenezi. Mitundu yonse ya anthu imayenda, uliwonse m'njira ya mulungu wake; koma ife tidzayenda m'njira ya Chauta, Mulungu wathu, mpaka muyaya. Chauta akunena kuti, “Pa tsiku limenelo, ndidzasonkhanitsa opuwala, ndidzakusa amene adachotsedwa kwao, ndiponso amene ndidaŵalanga. Opundukawo ndidzaŵasandutsa anthu anga otsala, amene adachotsedwa kwao ndidzaŵasandutsa mtundu wamphamvu. Ine Chauta ndidzakhala mfumu yao pa phiri la Ziyoni, kuyambira nthaŵi imeneyo mpaka muyaya. “Tsono iwe Ziyoni, nsanja yotetezera nkhosa zanga, phiri la anthu anga, zimene ndidaakulonjeza zidzachitikadi. Ufumu wako wakale uja udzakubwereranso, Anthu a ku Yerusalemu ufumu wao uja udzafikanso.” Kodi ukuliriranji mokuŵa chonchi mzinda iwe? Ukusaukiranji ngati mkazi pa nthaŵi yake yochira? Kodi ndiye kuti ulibe mfumu, kapena phungu wokulangiza? Muphiriphithe ndi kubuula, inu anthu a ku Ziyoni, ngati mkazi pa nthaŵi yake yochira. Pakuti tsopano mudzachoka mumzindamo, mukakhala mumidzi. Mudzachotsedwa kupita ku Babiloni. Komabe kumeneko mudzapulumutsidwa, kumeneko Chauta adzakuwombolani kwa adani anu. Tsopano mitundu yambiri yasonkhana kuti imenyane ndi iwe Ziyoni. Ikunena kuti, “Tiyeni timuipitse, tiwone kutha kwake kwa mzinda wa Ziyoniwu.” Koma anthuwo maganizo a Chauta saŵadziŵa, zimene Iye akukonzekera, iwo sazimvetsa. Sadziŵa kuti Iye waŵaunjika ngati mitolo ya tirigu pa malo opunthira. Yamba kupuntha iwe Ziyoni, ndidzakusandutsa wamphamvu ngati nkhunzi ya nyanga zachitsulo, ngati nkhunzi ya ziboda zamkuŵa. Udzatswanya mitundu yambiri ya anthu, zimene adapindula udzazipereka kwa Chauta, chuma chao udzachipereka kwa Ambuye a dziko lonse lapansi. Tsopano konzekani m'magulu ankhondo, inu a ku Yerusalemu. Atizinga ndi zithando zankhondo, akuthira nkhondo likulu la Israele. Chauta akuti, “Koma iwe Betelehemu wa ku Efurata, inde ndiwe wamng'ono pakati pa mafuko a Yuda, komabe mwa iwe ndidzatulutsa munthu amene adzakhala wolamulira Israele. Iyeyo chiyambi chake nchakalekale, cha masiku amakedzana.” Nchifukwa chake Mulungu adzasiya Israele mpaka pa nthaŵi yoti achire mkazi amene adzabale mwana. Pamenepo, otsala a mtundu wake adzabwereranso kwa Aisraele anzao. Iye adzalimbikira, ndipo adzaŵeta nkhosa zake mwa mphamvu za Chauta ndi ulemerero wa dzina la Chauta, Mulungu wake. Ndipo iwo adzakhala mu mtendere, poti ukulu wake udzakhazikika pa dziko lonse lapansi. Ndiye amene adzakhazikitse mtendere. Aasiriya akadzaloŵa m'dziko mwathu ndi kuyamba kutithira nkhondo, tidzaŵatumira atsogoleri ankhondo asanu ndi aŵiri kapena akalonga asanu ndi atatu. Iwowo adzagonjetsa dziko la Asiriya ndi lupanga, dziko la Nimirodi adzalilamulira mwankhondo. Adzatipulumutsa kwa Aasiriya, iwowo akadzakaloŵa m'dziko mwathu, kudzatithira nkhondo. Onse otsalira a Yakobe adzakhala dalitso pakati pa mitundu yambiri ya anthu ngati mame ochoka kwa Chauta. Adzakhala ngati mvula yowaza pa udzu, imene sichita kulamulidwa ndi anthu, siidikira lamulo la munthu. Onse otsalira a Yakobe adzakhala temberero pakati pa mitundu ya anthu, ngati mkango pakati pa nyama zam'nkhalango. Adzakhala ngati mwana wa mkango, pakati pa gulu la nkhosa, amene amati akadzaziloŵerera, amazimbwandira ndi kuzikadzula. Ndipo sipakhala wozipulumutsa. Inu Aisraele, mudzapambana adani anu, ndipo adani anu onsewo adzaonongeka. Komabe Chauta akuuza Aisraele kuti, “Pa tsiku limenelo ndidzaononga akavalo anu onse, ndipo ndidzaphwasula magaleta anu. Ndidzaononga mizinda ya m'dziko mwanu ndi kugwetseratu malinga anu. Ndidzasakaza masenga anu onse, ndipo pakati panu sipadzakhalanso oombeza. Ndidzaononga mafano anu onse pamodzi ndi miyala yoimika yopembedzerapo m'dziko mwanu. Simudzazigwadiranso zinthuzo zimene mudapanga ndi manja anu. Ndidzagwetsa mafano anu a Asera m'dziko mwanu, ndipo ndidzaononga mizinda yake. Mwaukali ndi mokwiya ndidzalanga mitundu yonse ya anthu imene sidandimvere.” Imvani tsopano zimene Chauta anene. Dzukani Ambuye, mufotokoze pamaso pa mapiri mlandu wanu. Magomo amve mau anu. Imvani mlandu wa Chauta, inu mapiri, ndi inunso maziko amuyaya a dziko lapansi. Chautatu akuimba mlandu anthu ake, akutsutsana ndi Aisraele. Chauta akuti, “Inu anthu anga, kodi ndakuchitani chiyani? Kodi ndakutopetsani nchiyani? Tandiyankhani! Paja Ine ndidakutulutsani ku dziko la Ejipito. Ndidakuwombolani ku dziko laukapololo. Ndipo ndidaachita kutuma Mose, Aroni ndi Miriyamu kuti akutsogolereni. Inu anthu anga, kumbukirani zimene Balaki, mfumu ya ku Mowabu, adaafuna kukuchitani, ndiponso m'mene Balamu mwana wa Beori adamuyankhira. Kumbukirani zimene zidachitika pa ulendo wochoka ku Sitimu kupita ku Giligala. Kumbukirani zonsezi kuti muzindikire zimene Ine Chauta ndidachita pofuna kukupulumutsani.” Kodi nditenge chiyani kuti ndifike pamaso pa Chauta, kuti ndikapembedze Mulungu Wakumwamba? Kodi nditenge anaang'ombe a chaka chimodzi kuti ndipereke nsembe zopsereza? Kodi Chauta adzakondwera ndi nkhosa zamphongo zikwi zingapo kapena mitsinje ya mafuta zikwi khumi? Kodi ndidzapereke mwana wanga wachisamba chifukwa cha zolakwa zanga? Kodi mwana wanga adzakhale nsembe yolipira tchimo langa? Iyai, Chauta adakuwonetsa kale, munthu iwe, chimene chili chabwino. Zimene akufuna kuti uzichita ndi izi: uzichita zolungama, uzikhala wachifundo, ndipo uziyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako. Ndi nzeru kuwopa dzina la Chauta. Akuuza mzinda wa Yerusalemu kuti, “Imvani, inu anthu onse okhala mumzinda muno. Kodi Ine ndingathe kuiŵala chuma chimene chili m'nyumba za anthu oipa, chimene adachipata monyenga, ndiponso muyeso wopereŵera umene uli wotembereredwa? Kodi ndingathe kulekerera munthu amene ali ndi sikelo zobera anzake ndiponso miyeso yonyenga? Anthu olemera amachita zankhondo. Anthu onse ndi abodza, amangokhalira kunama. Nchifukwa chake ndayambapo kukukanthani, kukuwonongani chifukwa cha machimo anu. Mudzadya, koma simudzakhuta. Njala sidzakuchokani. Mudzakundika zinthu, koma sizidzasungika. Zimene mudzakundika zidzaonongedwa pa nkhondo. Mudzabzala, koma simudzakolola, Mudzayenga mafuta a olivi, koma simudzaŵadzola. Mudzaponda mphesa, koma vinyo wake simudzamulaŵa. Mwasunga machitidwe oipa a mfumu Omuri ndi ntchito zonse za banja la Ahabu. Mwatsata njira zao zonse. Motero ndidzakuwonongani kotheratu. Anthu a mitundu ina adzakunyodolani, kulikonse anthu adzakunyozani.” Kalanga ine! Ndasanduka ngati wokunkha wosapeza zotsalira. Sipadatsalenso mphesa zoti nkudya. Sipadatsaleko nkhuyu zimene ndimazikonda. Anthu abwino atha pa dziko lapansi, palibe ndi mmodzi yemwe wolungama. Onse akubisalirana mwachiwembu. Aliyense akusakira mbale wake mu ukonde. Ndi akatswiri pochita zoipa. Akalonga ndi aweruzi amafuna ziphuphu, ndipo mtsogoleri amaŵauza zoipa zimene afuna kuti iwo achite. Motero amalakwira pamodzi. Munthu wabwino koposa ali ngati lunguzi, wolungama koposa ndi wolasa ngati tchinga laminga. Lafika tsiku la chilango, limene alonda ao, aneneri, adanena. Lafika tsiku la chisokonezo chao. Wina asakhulupirire mnansi, asadalire bwenzi lake lapamtima. Aliyense achenjere ndi pakamwa pake, ngakhale polankhula ndi mkazi wake yemwe. Makono ana aamuna akunyoza atate ao, ana aakazi akuukira amai ao. Mtengwa akulongolozana ndi mpongozi wake, nkhondo ndi anansi. Koma ine ndidzadalira Chauta. Ndidzaika mtima pa Mulungu Mpulumutsi wanga. Mulungu wanga adzandimva. Inu adani athu musatiseke. Tidagwa inde, koma tidzadzukanso. Ngakhale tikhale mu mdima, Chauta ndiye nyale yathu. Tachimwira Chauta, nchifukwa chake tiyenera kupirira mkwiyo wake, mpaka atazenga mlandu wathu ndi kuugamula. Koma pambuyo pake adzatiloŵetsa m'kuŵala, ndipo tidzaona chipulumutso chake. Tsono adani athu adzaona zimenezi, ndipo manyazi adzaŵagwira anthu amene ankatifunsa kuti, “Ali kuti Chauta, Mulungu wanu?” Tidzaona kugonjetsedwa kwao, adzaponderezedwa ngati matope m'miseu. Inu anthu a ku Yerusalemu, idzafikatu nthaŵi yomanganso malinga anu. Nthaŵi imeneyo malire anu adzafutuzidwa. Nthaŵi imeneyo anthu anu adzabwerera kwa inu kuchokera ku Asiriya mpaka ku Ejipito, kuchokera ku Ejipito mpaka ku Mtsinje wa Yufurate, ndiponso kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja inanso, kuchokera ku phiri lina mpaka ku phiri linanso. Koma dziko lapansi lidzasanduka chipululu chifukwa cha zoipa za anthu ake. Amenewo ndiwo malipiro a ntchito zao. Inu Chauta muŵatsogolere anthu anu ndi ndodo yanu yoŵatetezera, muŵete nkhosa zanu zimene mudazisankha. Tsopano zikukhala zokha m'nkhalango pakati pa dziko la chonde. Koma muzilole kuti zikadye ku busa labwino, ku Basani ndi Giliyadi, monga masiku akale. Chauta akuti, “Ndidzaŵaonetsa zodabwitsa, monga masiku amene ankatuluka ku Ejipito.” Anthu a mitundu yambiri akadzaona zimenezo adzachita manyazi, ngakhale ali ndi mphamvu zotani. Adzangogwira pakamwa, ndi kutseka makutu motaya mtima. Adzavimvinizika pa dothi ngati njoka, ngati zolengedwa zina zokwaŵa. Adzabwera ali njenjenje kuchokera ku malinga ao. Moopa adzatembenukira kwa Inu Chauta, Mulungu wathu, ndipo adzachita nanu mantha. Kodi ndani ali Mulungu ngati Inu, amene amakhululukira machimo ndi kuiŵala zolakwa za anthu anu otsala? Simusunga mkwiyo mpaka muyaya, chifukwa muli ndi chikondi chosasinthika. Mudzatichitiranso chifundo. Mudzapondereza pansi zolakwa zathu, mudzataya machimo athu onse pansi pa nyanja. Mudzaonetsa kukhulupirika kwanu kwa Yakobe, ndi chikondi chanu chosasinthika kwa Abrahamu, monga mudalonjezera molumbira kwa makolo athu kuyambira pa masiku amakedzana. Uwu ndi uthenga wonena za mzinda wa Ninive. Uthengawu ukufotokoza za zimene Nahumu wa ku Elikosi adaziwona m'masomphenya. Chauta ndi Mulungu wansanje ndiponso wolipsira. Chauta amalanga, ndipo ndi wamkali. Chauta amalipsira amaliwongo ake amakwiyira adani ake. Chauta ndi wamphamvu zedi. Ndi wosakwiya msanga, komabe sadzalola kuti munthu wochimwa akhale wosalangidwa. Pamene amayenda pamachitika kamvulumvulu ndi mphepo yamkuntho, mitambo ndiye fumbi limene mapazi ake amachititsa. Akangoilamula nyanja, imauma, amaumitsanso mitsinje yonse. Zomera za ku Basani ndi za ku Karimele zimauma, maluŵa a ku Lebanoni amafota. Mapiri amagwedezeka pamaso pake, magomo amasungunuka. Dziko lapansi limanjenjemera pamaso pake, ndiye kuti dziko ndi zonse zokhala m'menemo. Kodi ndani angathe kuima pamaso pa Chauta, Iye atakwiya? Kodi ndani angathe kupirira ukali wake? Ukali wake umayaka ngati moto, matanthwe amadyukuka pamaso pake. Chauta ndi wabwino, ndiye kothaŵira pa nthaŵi yamavuto. Amasamala onse amene amadalira Iye. Koma ndi madzi achigumula adzaononga adani ake, ndipo adzaŵapirikitsira ku malo amdima. Kodi mukukonzekera kumchita Chauta chiwembu chotani? Adzakuwonongani kotheratu. Sadzalira kuŵalipsira kaŵiri adani akewo. Adzaŵatentha kotheratu ngati ziyangoyango za minga ndiponso ngati ziputu zouma. Ku Ninive kudachokera munthu wa cholinga choipa, wofuna kuchita Chauta chiwembu. Zimene akunena Chauta ndi izi, akuti, “Ngakhale Aasiriyawo ndi amphamvu ndiponso ndi ambiri, adzaonongeka ndi kutheratu. Koma inu anthu anga, ngakhale ndidakulangani, sindidzakulanganinso. Tsopano ndidzathyola goli limene adakuikani m'khosi, ndipo ndidzadula maunyolo anu.” Za inu a ku Ninive Chauta walamula kuti, “Simudzakhala ndi adzukulu otchedwa dzina lanu. Ndidzaononga mafano osema ndi oumba m'nyumba ya milungu yanu. Ndidzakukumbirani manda, chifukwa ndinu opandapake.” Ona, kumapiri kukubwera munthu, iyeyu ali ndi uthenga wabwino, akulengeza za mtendere. Inu a ku Yuda muzisunga masiku achikondwerero; zimene mudalumbira, muzizichitadi. Anthu oipawo sadzakuthiraninso nkhondo. Adaonongeka kotheratu. Inu a ku Ninive, othira nkhondo akubwera kudzakuwonongani. Ikani ankhondo pa malinga! Muziyang'ana ku mseu! Konzekerani nkhondo! Valani dzilimbe! Patsala pang'ono kuti Chauta abwezere ulemerero wa Israele, monga udaaliri kale, ofunkha asanalande zinthu zonse ndi kuwononga mphesa zao. Zishango za ankhondo ao nzofiira, asilikali ao onse avala zovala zamlangali. Atandanda pa mizere yankhondo, magaleta ao akuchezimira ngati malaŵi a moto. Akavalo akungoti jodojodo. Magaleta akuthamanga m'miseu. Ali piringupiringu m'mabwalo. Ali ŵaliŵali ngati miyuni yoyaka. Ali ng'aning'ani ngati mphezi. Atsogoleri a ankhondo akuitanidwa, akubwera naphunthwa. Akuthamangira ku linga la mzinda, akuimika chipupa chodzitetezera. Akutsekula zipata zotchinga dziŵe la madzi, kunyumba kwa mfumu kwadzaza mantha. Mfumukazi yake yatengedwa ukapolo. Adzakazi ake akulira ngati nkhunda, ndipo akudzigunda pa chifuwa. Ninive wasanduka ngati chidziŵe, chimene madzi ake ali faa kutuluka. Ena akufuula kuti, “Imani! Imani!” Koma palibe amene akubwerera. Funkhani siliva! Funkhani golide! Chuma chake nchosatha, za mtengo wapatali nzosaŵerengeka. Mzinda wa Ninive waonongeka, wasanduka bwinja, wopanda anthu. Mitima yachokamo, maondo akuwombana, m'nkhongono muli zii, nkhope zasinthika ndi mantha. Kodi tsopano mzinda uja uli kuti? Unali ngati phanga la mikango, m'mene ana ake ankadyeramo, m'mene mikango yonse inkakhala mopanda mantha. Mkango wamphongo unkapha nyama yokwanira mkango waukazi ndi ana ake. Unkadzaza phanga lakelo ndi nyama yokadzulakadzula. Chauta Wamphamvuzonse akuuza a ku Ninive kuti, “Ine sindikugwirizana nanu, ndidzakutentherani magaleta anu. Lupanga lidzakuwonongerani ankhondo anu amene ali ngati mikango. Ndidzakulandani zonse zimene mudafunkha pa dziko lapansi. Amithenga anu sadzamvekanso mau.” Tsoka kwa mzinda wokhetsa magazi a anthu ambiri, mzinda wodzaza ndi mabodza ndi zakuba, wokonda kufunkha mosalekeza. Imvani kulira kwa zikoti, kukokoma kwa mikombero, likitilikiti wa akavalo ndi kulilima kwa magaleta. Okwera pa akavalo akuthamanga, malupanga ali ŵaliŵali, mikondo ili phuliphuli. Afa anthu ambiri, mitembo yati vuu, yosaŵerengeka, anthu kumaphunthwa pa mitemboyo. Zonsezo zachitika chifukwa cha zonyansa zochuluka za Ninive, mkazi wachiwerewere uja. Ankakopa anthu ndi kukongola kwake konyenga. Ankanyengadi anthu a mitundu yonse ndi zadama zake nakopa mafuko ndi zithumwa zake. Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Ine sindikugwirizana nawe, ndidzakuvula ndi kukunyazitsa. Anthu a mitundu yonse adzaona maliseche ako, udzachita manyazi pamaso pa maiko onse. Ndidzakuthira zonyansa, ndidzakunyodola, ndipo ndidzakusandutsa chinthu chomachiseka. Ndipo onse okuwona adzakuthaŵa, adzati, ‘Ninive wasanduka bwinja, adzamlira ndani?’ Ndidzamtenga kuti woti akusangalatse?” Akuterotu Chauta. Kodi iwe Ninive ndiwe wopambana Thebesi? Suja mzinda umenewu unali m'mbali mwa mtsinje wa Nailo utazingidwa ndi madzi. Madziwo anali ngati khoma lake ndi linga lake? Mzindawo unkalamulira Etiopiya ndi Ejipito, mphamvu zake zinali zopanda malire. Aputi ndi Alibiya ndiwo ankagwirizana nawo. Komabe anthu a ku Thebesi adagwidwa, adasanduka akapolo. Ana ao adaŵakankhanthitsa pansi m'miseu yonse ya mumzindamo. Adani adagaŵana anthu otchukawo mwamaere. Akuluakulu onse adaŵamanga ndi maunyolo. Iwenso Ninive udzachita ngati waledzera, mutu wako udzazungulira. Nawenso udzafunafuna malo othaŵirako. Malinga ako onse adzakhala ngati mitengo ya nkhuyu zoyamba kupsa. Akaigwedeza, nkhuyuzo zimagwera m'kamwa mwa wofuna kuzidya. Ankhondo ako ali ngati akazi. Zipata za dziko lako zaŵatsekukira adani ako, ndipo moto wapsereza mipiringidzo yake. Mutungiretu madzi kuti adzakwanire pa nthaŵi yokuzingani, limbitsani malinga anu. Pondani dothi, ponyani m'chikombole, ndipo muumbe njerwa. Ngakhale mutero, moto udzakupserezanibe, ndipo lupanga lidzakukanthani, mudzapululuka ngati dzombe. Swanani ngati dzombe, chulukanani ngati ziwala. Mudachulukitsa anthu anu amalonda kupambana nyenyezi zamumlengalenga. Koma onsewo adamwazikana ngati dzombe. Nduna zanu zili ngati dzombe. Akuluakulu anu ali ngati ziwala, zimene zimangokangamira pa khoma kukazizira. Koma dzuŵa likamatuluka, zimauluka, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene amadziŵa kumene zapita. Iwe mfumu ya Aasiriya, nduna zako zaferatu. Akuluakulu ako apitiratu. Anthu ako amwazikira ku mapiri, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe woŵasonkhanitsa. Palibe mankhwala a bala lako, chilonda chako sichingapole. Onse amene amamva za iwe, amaomba m'manja mokondwa. Kodi alipo wina amene sadazilaŵepo nkhanza zako zosathazi? Uwu ndi uthenga umene mneneri Habakuku adalandira kwa Mulungu m'masomphenya. Kodi Inu Chauta, ndidzakhala ndikukupemphani chithandizo nthaŵi yaitali bwanji, Inuyo osandiyankha? Kapena kukudandaulirani kuti “Nkhondo kuno,” Inuyo osatipulumutsa? Chifukwa chiyani mukufuna kuti ndiziwona mavuto otereŵa. Chifukwa chiyani mukulekerera zoipa? Ponseponse ndikuwona chiwonongeko ndiponso nkhondo. Pali ndeu ndi kukangana kwambiri. Ndiye kuti malamulo atha mphamvu. Chilungamo sichikugwira ntchito. Anthu oipa akupambana anthu abwino, motero chilungamo chalephereka. Onani mitundu ya anthuyi, muipenyetsetse. Kudzakhala zododometsa ndipo mudzangoti kakasi. Pakuti ndidzachita zinthu zimene simudzakhulupirira mukadzazimva. Ndiye kuti ndidzakweza Ababiloni mtundu woopsa ndi wamphamvu. Iwowo amapita pa dziko lonse lapansi kuti akalande malo a eniake. Kulikonse kumene amapita, amachititsa mantha, amadzipangira okha malamulo, amadzipezera okha ulemu. Akavalo ao ndi aliŵiro kwambiri kupambana akambuku, ndi oopsa kupambana mimbulu yolusa. Okwerapo ao akuthamanga molunjika kuchokera kutali. Akuchita kugudukira ngati chiwombankhanga chofuna kugwira nyama. Gulu lao lankhondo likubwera ndi nkhanza, anthu akuchita mantha iwo asanafike. Amagwira akapolo ochuluka ngati mchenga. Amanyoza mafumu, amanyazitsa atsogoleri. Amapeputsa linga lililonse, poti amangounjika dothi lokwererapo, nalanda mzinda wake. Kenaka amapitirira mofulumira ngati mphepo. Anthuwo amene mphamvu ndiye mulungu wao. Inu Chauta, kodi suja ndinu wachikhalire? Ndinu Mulungu wanga, Woyera wanga uja, wosafa. Inu Chauta, ndinu amene mudaŵasankha anthuwo kuti abweretse chiweruzo pa ife. Inu Thanthwe lathu, mudaŵaika iwowo kuti atilange. Maso anu ndi oyera, safuna kuwona zoipa, simungalekerere anthu ochita uchimo ndi zolakwa. Chifukwa chiyani nanga mukulekerera anthu osakhulupirikawo? Bwanji simuchitapo kanthu pamene anthu oipa akuwononga anthu abwino kupambana iwowo? Mumasandutsa anthu kuti azikhala ngati nsomba zam'nyanja, ngati zokwaŵa zimene zilibe wozilamulira? Adani ao amachita ngati kuŵedza anthuwo ndi mbedza, kapena kuŵakola m'kombe. Amaŵakokera m'matchera ao, ndipo amakondwa ndi kusangalala. Tsono amaperekera nsembe makombe ao, ndipo amafukizira lubani matchera ao. Chifukwa zimenezi ndizo zimaŵabweretsera moyo wapamwamba, ndipo amadya bwino. Kodi adzapitirirabe kugwiritsa ntchito makoka ao, ndi kumapha mitundu ya anthu mopanda chifundo mpakampaka? Ndidzakhala ngati mlonda, woimirira pa linga. Ndidzaona zimene adzandiwuze, apo ndidzadziŵa zimene adzayankhe za dandaulo langa. Chauta adandiyankha kuti, “Lemba uthengawu, ulembe mooneka bwino pa mapale, kuti woŵerenga aŵerenge mosavuta. Uthengawu ukudikira nthaŵi yake. Nthaŵi yakeyo idzabwera mofulumira, sizidzalephera kuchitika. Ngati ziwoneka kuti zikuchedwa, mudikire. Zidzafika ndithu, si kuchedwa ai. Ochita zoipa adzalephera, koma ochita chifuniro cha Chauta adzakhala ndi moyo chifukwa cha kukhulupirika kwake. Monga munthu wokhuta vinyo ali wosokonezeka, chonchonso munthu wodzitama ndi wosakhazikika. Ndi waumbombo kwambiri ngati manda, ngati imfa amakhala wosakhuta. Amagwira anthu a mitundu yonse, amaŵasonkhanitsa ngati ake.” Koma ogwidwawo adzamnyoza, adzamnyodola ponena kuti, “Tsoka kwa amene amadzikundikira chuma chosakhala chake, amene amalemera ndi ngongole zosalungama. Adzatero mpaka liti?” Angongolewo adzakuukira mwadzidzidzi. Adzakuchititsa mantha ndi kukulanda zako zonse. Chifukwa iweyo udafunkha mitundu yambiri ya anthu, koma otsala adzakufunkha iweyo, chifukwa chokhetsa magazi a anthu ambiri, ndiponso chifukwa choononga mwankhanza mizinda ndi onse okhalamo. Tsoka kwa amene amalemera ndi phindu lobera anzake, kuti akweze malo ake ndi kupewa zovuta. Udafuna kuwononga anthu a mitundu yambiri koma potero wachititsa manyazi banja lako, ndipo wataya moyo wako. Ndi njerwa zomwe za nyumba yako zidzafuula chidzudzulo, ndipo mitanda idzathira mang'ombe ake. Tsoka kwa amene wamanga mzinda pokhetsa magazi, ndipo waukhazikitsa pozunza anthu. Koma Chauta Wamphamvuzonse ndiye watsimikiza kuti zimene anthu amagwirira ntchito zili ngati nkhuni pa moto. Anthu a mitundu yonse amangodzitopetsa popanda phindu. Motero anthu onse adzazindikira ulemerero wa Chauta kuti ndi wodzaza, monga momwe madzi amadzazira nyanja. Tsoka kwa amene amamwetsa anzake zaukali, amene amaŵaledzeretsa kuti aŵachititse manyazi. Koma amene udzachite manyazi ndiwe ndipo onse adzakunyoza kwambiri. Tsopano imwa ndiwe, mpaka kudzandira. Chikho cha chilango cha Chauta chikupeza, ndipo manyazi adzaphimba ulemerero wako. Udzachita mantha chifukwa cha kusakaza nkhalango za ku Lebanoni. Udzaopsedwa chifukwa cha kuwononga nyama zake. Wakhetsa magazi a anthu mwankhanza, waononga mizinda ndi onse okhalamo. Kodi phindu la fano nchiyani? Adalipanga ndi munthu. Ndi chifanizo chabe, ndipo nchinthu chonyenga. Munthu wopangayo amakhulupirira zimene wachita, koma mafano akewo satha nkulankhula komwe. Tsoka kwa amene amauza mtengo kuti, “Nyamuka!” Amene amauza mwala waduu kuti, “Dzuka!” Kodi zimenezi zingathe kulangiza? Nzopangidwa ndi golide ndi siliva, ndipo sizitha konse kupuma. Koma Chauta ali m'Nyumba yake yoyera. Dziko lonse lapansi likhale chete pamaso pake. Pemphero la mneneri Habakuku potsata maimbidwe a Sigionoti. Inu Chauta, ndamva za mbiri yanu, Inu Chauta, ntchito zanu zandiwopsa. Muzichitenso masiku ano, zikhale zodziŵika makono. Ngakhale muli okwiya, musaiŵale chifundo chanu. Mulungu adabwera kuchokera ku Temani, Woyera uja adabwera kuchokera ku phiri la Parani. Ulemerero wake udaphimba mlengalenga, dziko lonse lapansi linkamutamanda. Adaŵala ngati dzuŵa, kunyezimira kunkatuluka m'manja mwake, m'mene adabisamo mphamvu zake. Kutsogolo kwake kudagwa mliri, kumbuyo kwake kudagwa nthenda yoopsa. Adaimirira ndipo dziko lapansi lidagwedezeka. Adayang'ana ndipo mitundu ya anthu idanjenjemera. Pomwepo mapiri okhazikika adagumuka, ndipo magomo akalekale adatera, njira zake nzachikhalire. Ndidaona anthu a ku Kusani ali pa mavuto, nawonso a ku Midiyani adaagwedezeka. Inu Chauta, kodi mudaakwiyira mitsinje? Kodi mudaakalipira mifuleni? Kodi mudaazazira nyanja? Mutakwera pa akavalo anu mudapambanitsa anthu anu pa nkhondo. Mudasolola uta wanu m'chimake, ndipo mudatulutsa mivi m'phodo lake. Mudang'amba dziko lapansi ndi mitsinje. Mapiri atakuwonani adayamba kugwedezeka. Madzi amphamvu am'mitsinje adasefukira. Nyanja yozama idakokoma, mafunde ake adakwera kwambiri. Dzuŵa ndi mwezi zidangoti jega mu mlengalenga, zitaona kung'anipa kwa mivi yanu, ndi kunyezimira kwa mikondo yanu. Mudayendayenda m'dziko lapansi muli okwiya, mudapondereza anthu a mitundu yonse mwaukali. Mudapita kukapulumutsa anthu anu, mudabwera kudzalanditsa wodzozedwa wanu. Mudakantha mtsogoleri wa dziko la anthu oipa, mudaonongeratu anthu ake onse. Ndi mivi yanu mudalasa mtsogoleri wa ankhondo ake, amene adaabwera ngati kamvulumvulu kuti atibalalitse. Ankakondwerera ngati kuti akudzaononga osauka mwachinsinsi. Mudapondaponda pa nyanja ndi akavalo anu, ndipo madzi amphamvu adavwanduka. Izi ndazimva, ndipo thupi langa likunjenjemera, m'kamwa fuu chifukwa cha phokosolo. M'mafupa mwazizira, ndipo maondo akuwombana. Ndikudikira tsiku la chilango chimene chidzagwera amene akutithira nkhondo. Ngakhale mikuyu ipande kuchita maluŵa, mipesa ipande kukhala ndi mphesa, mitengo ya olivi ipande kubala zipatso, m'minda musatuluke kanthu, ndipo nkhosa ndi ng'ombe zithe m'khola, komabe kwanga nkukondwerera mwa Chauta, kwanga nkusangalala chifukwa cha Mulungu Mpulumutsi wanga. Ambuye anga, Chauta, ndiwo amandipatsa mphamvu. Amalimbitsa miyendo yanga kuti ikhale ngati ya mbaŵala, kuti ndikafike mpaka pamwamba pa phiri. Kwa Woimbitsa nyimbo. Aimbire zazingwe. Pa nthaŵi ya Yosiya, mwana wa Amoni, mfumu ya ku Yuda, Chauta adamupatsa uthenga Zefaniya, mwana wa Kusi, mwana wa Gedaliya, mwana wa Amariya, mwana wa Hezekiya. Chauta adati, “Ndidzafafaniziratu zonse za pa dziko lapansi.” “Ndidzafafaniziratu anthu ndi nyama zomwe. Ndidzaononga mbalame zamumlengalenga ndi nsomba zam'nyanja. Ndidzagwetsa anthu ochimwa. Ndidzafafaniziratu mtundu wa anthu kuti usaonekenso pa dziko lapansi,” akuterotu Chauta. “Ndidzasamula dzanja langa kuti ndilange anthu a m'dera la Yuda ndi onse okhala ku Yerusalemu. Ndidzafafaniziratu zotsalira zonse za Baala pa malo ano. Palibe aliyense amene adzakumbukirenso ansembe a fanolo. Ndidzafafanizanso amene amaŵerama pa madenga ao nkumapembedza dzuŵa, mwezi ndi nyenyezi. Ndidzaononganso amene amati kwinaku akulambira Chauta ndi kulumbira m'dzina lake, kwinaku nkumalumbira m'dzina la Milikomu. Iwowo adafulatira Chauta osamtsatanso, safuna kupembedza Chauta, kapena kumpempha nzeru.” Khalani chete pamaso pa Ambuye Chauta! Tsikutu la Chauta layandikira. Chauta wakonza kuti anthu ake adzaperekedwe ngati nsembe, ndipo wapatuliratu oitanidwa odzapereka nsembeyo. Chauta akuti, “Pa tsiku limenelo la nsembe yanga ndidzalanga ana a mfumu ndi akalonga ake, ndi onse otengera zachilendo. Pa tsiku limenelo ndidzalanga onse olumpha pa chiwundo, ndiponso amene amachita zankhanza ndi zonyenga zambiri.” Chauta akunena kuti, “Pa tsiku limenelo kulira kwakukulu kudzamveka ku Chipata cha Msika wa Nsomba; kulira kwakukuluko kudzamveka ku chigawo cham'kati cha mzinda wa Yerusalemu; kudzamvekanso kugunda kuchokera ku mapiri. Inu okhala ku chigwa cha mzinda lirani komvetsa chisoni, chifukwa amalonda onse atha, onse ogulitsa siliva aonongeka. Pa nthaŵi imeneyo ndidzafufuzafufuza mu Yerusalemu ndi nyale, ndipo ndidzaŵalanga anthu ongokhala khale ngati vinyo wosakhutchumula, amene mumtima mwao amati, ‘Chauta sadzachitapo chabwino, kapena kuchitapo choipa.’ Anthu otereŵa chuma chao adani adzachifunkha, nyumba zao adzaziphwasula. Adzamanga nyumba, koma sadzakhalamo. Adzabzala mphesa, koma sadzamwa vinyo wake.” Tsiku lalikulu la Chauta lili pafupi, layandikira ndipo likudza mofulumira. Tsikulo kubwera kwake nkopweteka, ngakhale ankhondo amphamvu omwe akulira pamenepo. Tsikulo lidzakhala tsiku la mkwiyo wa Chauta, tsiku la mavuto ndi mazunzo, tsiku la kuwonongeka ndi kupasuka kwa zinthu, tsiku la mdima ndi chisoni, tsiku la mitambo ndi labii kuda. Tsiku limenelo kudzamveka lipenga ndi kufuula kwankhondo, kwa asilikali othira nkhondo mizinda ya malinga ndiponso nsanja zankhondo za Yerusalemu. Chauta akuti, “Chifukwa anthuwo adandichimwira, ndidzaŵasautsa koopsa, kotero kuti azidzayenda ngati akhungu. Magazi ao adzachita kuti mwaa ngati fumbi, matupi adzangoti vuu, nkumaola ngati ndoŵe. Ngakhale siliva wao kapena golide wao sadzatha kuŵaombola, tsiku la mkwiyo wa Chautalo. Ukali wake wotentha ngati moto, udzapsereza dziko lonse, ndipo mwadzidzidzi adzathetsa onse okhala m'menemo.” Inu anthu opanda manyazinu, chitani msonkhano, mulape, adani asanakumwazeni ngati mungu, ukali woopsa wa Chauta usanakugwereni, tsiku la mkwiyo wa Chauta lisanakupezeni. Funafunani Chauta, inu nonse odzichepetsa, inu amene mumamvera malamulo ake. Chitani zolungama, khalani odzichepetsa. Mwina mwake mudzatha kupulumuka pa tsiku la mkwiyo wa Chauta. Mzinda wa Gaza udzasiyidwa, Asikeloni adzasanduka bwinja. Anthu a ku Asidodi adzapirikitsidwa masana mwadzidzidzi, Akeroni adzapasuka. Tsoka kwa inu okhala m'mbali mwa nyanja, inu mtundu wa Akeretinu Mau a Chauta akukudzudzulani, inu anthu a ku Kanani, dziko la Afilisti, akuti, “Ndidzakuwonongani nonse sipadzatsala ndi mmodzi yemwe.” Dziko limene lili m'mphepete mwa nyanja, lidzasanduka madambo a abusa, ndi makola a nkhosa. Kumeneko kudzakhala dziko la otsala a m'banja la Yuda. Azidzadyetsa nkhosa zao m'mbali mwanyanjamo, ndipo madzulo azidzagona ku nyumba za ku Asikeloni. Pakuti Chauta, Mulungu wao adzaŵasamalira, ndiye amene adzaŵabwezere ufulu wao. Chauta akuti, “Ndamva kunyoza kwa Amowabu, ndiponso kutukwana kwa Aamoni, m'mene anyozera anthu anga ndi m'mene adzikuzira m'dziko mwao. Nchifukwa chake Ine Chauta Wamphamvuzonse ndikulumbira kuti, Pali Ine ndemwe, Mulungu wamoyo wa Israele, Amowabu adzaonongedwa ngati anthu a ku Sodomu, Aamoni adzaonongedwa ngati anthu a ku Gomora. Malowo adzakhala ngati dera la zitsamba za khwisa ndi la nkhuti za mchere, dziko lachipululu mpaka muyaya. Otsala mwa anthu anga adzafunkha malowo. Opulumuka a mtundu wanga adzalandira malowo ngati dziko lao.” Chimenechi chidzakhala chilango choyenerera kunyada kwaoko, chifukwa adanyoza anthu a Chauta Wamphamvuzonse. Motero Chauta adzaŵaopsa kwambiri. Adzaononga milungu yonse ya pa dziko lapansi. Mitundu yonse ya anthu idzampembedza Chauta, mtundu uliwonse ku dziko lakwao. Inunso Aetiopiya, Chauta adzakukanthani ndi lupanga lake. Chauta adzasamulira dzanja lake kumpoto ndi kuwononga dziko la Asiriya. Mzinda wa Ninive adzausandutsa bwinja, udzakhala wagwaa ngati chipululu. Choncho zoŵeta zizidzagona kumeneko chimodzimodzinso nyama zonse zakuthengo. Adembo ndi akanungu azidzagona pa makapotolosi ake. Akadzidzi azidzalira pa windo, ndipo makwangwala azidzakhala pa bwalo lake. Mitengo yake yamkungudza adzaisadza. Umenewo ndiwo mzinda umene unkadzimva kuti ndi wokhazikika, umene mumtima mwake unkati, “Ine pano! Palibenso wina ai!” Tauwonani m'mene wasakazikira tsopano! Wasanduka bwinja lokhalamo nyama zakuthengo. Aliyense wodutsamo azidzangotsonya nkumapukusa mutu. Tsoka kwa Yerusalemu, mzinda wopanduka, wonyansa ndi wankhanza. Sudamvere mau ouchenjeza. Sudasamale mau oudzudzula. Sudakhulupirire Chauta kapena kuyandikira kwa Mulungu wake. Nduna zake zinkakhuluma m'kati mwake, ngati mikango yobangula. Oweruza ake anali ngati mimbulu yoyenda madzulo, yosasiyako ndi fupa lomwe kuti lifike mpaka m'maŵa. Aneneri ake anali achabechabe, anthu osakhulupirika. Koma Chauta ndi wolungama mumzindamo, Iyeyo salakwa. Amaweruza molungama tsiku ndi tsiku, nthaŵi zonse salephera, koma osalungama akuchitabe zoipa opanda manyazi. Chauta akuti, “Ndaononga mitundu yonse ya anthu ndipo malinga ao onse ankhondo ndaŵaphwasula. Miseu yao ndaifafaniza palibenso anthu oyendamo. Mizinda yao yachitika bwinja, mulibe munthu ndi mmodzi yemwe wotsalamo. Ndidaaganiza kuti ndithudi anthu anga andiwopa, kuti avomera malango anga, ndipo kuti saiŵala malamulo anga. Koma ndi pamene iwo adanyanyira kumachita zoipa pa zochita zao zonse.” Chauta akunena kuti, “Nchifukwa chake mundidikire, mudikire tsiku limene ndidzakuimbeni mlandu. Pakuti ndatsimikiza zosonkhanitsa mitundu ya anthu pamodzi ndi maufumu onse, kuti ndiŵaonetse kusakondwa kwanga amve ululu wa ukali wanga. Dziko lonse lapansi lidzapserera ndi moto waukali wa mkwiyo wanga.” “Pamenepo ndidzasintha malankhulidwe a mitundu yonse, nkuŵapatsa malankhulidwe abwino, kuti onse azitama dzina la Chauta mopemba ndi kumamtumikira mogwirizana. Ngakhale kutali kutsidya kwa mitsinje ya ku Etiopiya, anthu ondipembedza, anthu anga obalalika, adzapereka nsembe kwa Ine.” “Tsiku limenelo inu a ku Yerusalemu simudzachitanso manyazi, chifukwa cha zoipa zonse zimene mudandichita, zimene mudandipandukira nazo. Pakuti nthaŵi imeneyo ndidzakuchotserani onse odzikuza ndi onyada. Simudzachitanso zonyada zanuzo pa phiri langa loyera. Pakati panu ndidzasiya anthu odzichepetsa ndi otsika. Iwowo adzafunafuna populumukira m'dzina la Chauta. Otsala a mu Israeleŵa sadzalakwanso, sadzalankhulanso zabodza, sadzachitanso zonyenga, Adzakhala pabwino mwamtendere, popanda wina woŵaopsa.” Imbani mokweza, inu anthu a ku Ziyoni! Fuulani inu Aisraele! Sangalalani, kondwani ndi mtima wonse, inu okhala mu Yerusalemu. Chauta wachotsa chilango chanu. Wapirikitsa adani anu. Chauta, Mfumu ya Israele, ali nanu pamodzi. Simudzaopanso choipa chilichonse. Tsiku limenelo adzauza Yerusalemu kuti, “Usaope, iwe Ziyoni, usataye mtima. Chauta, Mulungu wako, ali nawe pamodzi, ngati wankhondo wokuthandiza kugonjetsa adani. Adzasangalala ndi chimwemwe chifukwa cha iwe. Adzakubwezera m'chikondi chake. Adzakondwera nawe poimba nyimbo zachimwemwe. Monga pa masiku achikondwerero, ndidzakuchotsera tsoka, limene lingokuvutitsa ndi kukunyozetsa. Nthaŵi imeneyo ndidzaŵakhaulitsa onse amene amakuzunzani. Ndidzapulumutsa otayika ndi kusonkhanitsa onse obalalika. Ndidzaŵatamanda ndi kuŵapatsa ulemu, kulikonse kumene adani ao ankaŵachititsa manyazi. Nthaŵi imeneyo ndidzakusonkhanitsani, Ndidzakubwezerani kwanu. Ndidzakusandutsani otchuka ndi olemekezeka, pakati pa anthu a mitundu yonse ya pa dziko lapansi. Ndidzakubwezerani ufulu wanu inu mukupenya. Ndatero Ine Chauta.” Chaka chachiŵiri cha ufumu wa Dariusi, tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chimodzi, Chauta adapatsa mneneri Hagai uthenga. Uthengawu, wopita kwa Zerubabele mwana wa Salatiyele, bwanamkubwa wa ku Yuda, ndiponso kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, udati, “Zimene ndikunena Ine Chauta Wamphamvuzonse ndi izi: Anthu aŵa amanena kuti, ‘Nthaŵi siinafike yoti nkumanganso Nyumba ya Chauta.’ ” Tsono Chauta adapatsa mneneri Hagai uthenga uwu wakuti: “Kodi nzabwino zimenezi kuti inuyo muzikhala m'nyumba zomanga bwino, pamene Nyumba yangayi ili bwinja? “Nchifukwa chake tsono Ine Chauta Wamphamvuzonse ndikunena kuti muganizepo bwinotu pamenepa. Mwafesa zambiri, koma mwakolola pang'ono. Mumadya, koma osakhuta. Mumamwa, koma ludzu osatha. Mumavala, koma osamva kufunda. Malipiro a anthu antchito ndi osakwanira mpang'ono pomwe, “Nchifukwa chake Ine Chauta Wamphamvuzonse ndikunena kuti muganizeponso bwinotu pamenepa. Kwerani ku mapiri, mukadule nsichi, mudzandimangire Nyumba yoyenera, kuti ndikondwere nayo ndi kulandiriramo ulemerero. “Mwakhala mukuyembekeza zokolola zambiri, koma mwangopeza pang'ono. Pamene munkatuta zokolola zanu, Ine ndidangozimwazamwaza. Tsono Ine Chauta Wamphamvuzonse ndikuti, Ndidachitiranji zimenezi? Chifukwa chake nchakuti Nyumba yanga ndi bwinja, pamene aliyense akutanganidwa nkumanga nyumba yake. Nkuwonatu mvula yati zii, nthaka yati gwa. Nkuwonanso ndagwetsa chilala pa dziko lonse, pa minda ya tirigu, ya mphesa ndi ya mitengo ya olivi, pa zonse zomera pa nthaka, ndi pa zonse zimene anthu amalima, ndiponso pa anthu ndi nyama zomwe.” Pamenepo Zerubabele mwana wa Salatiyele, Yoswa mwana wa Yehozadaki mkulu wa ansembe, ndi anthu ena onse obwerako ku ukapolo, adachita zimene Chauta Mulungu wao adanena. Adamva mau a mneneri Hagai amene Chauta adamtuma, ndipo adachita mantha kwambiri. Motero Hagai, wamthenga uja, adaŵauza mau a Chauta akuti, “Ine Chauta ndikukuuzani kuti ndili nanu ndithu.” Tsono Chauta adalimbitsa mtima Zerubabele mwana wa Salatiyele, bwanamkubwa wa ku Yuda, ndi Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndiponso anthu ena onse. Adabwera, nayamba kugwira ntchito yomanga Nyumba ya Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wao, pa tsiku la 24 la mwezi wachisanu ndi chimodzi, wa chaka chachiŵiri pamene Dariusi anali mfumu. Chaka chachiŵiri cha ufumu wa Dariusi, pa tsiku la 21, mwezi wachisanu ndi chiŵiri, Chauta adapatsa mneneri Hagai uthenga. Uthengawu, wopita kwa Zerubabele mwana wa Salatiyele, bwanamkubwa wa ku Yuda, kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, ndiponso kwa ena onse, udati, “Kodi alipo ena mwa inu amene adaaona ulemerero wakale wa Nyumba iyi? Monga simukuwona kuti tsopano ulemererowo watheratu? Komabe Ine Chauta Wamphamvuzonse ndikuti, usataye mtima iwe Zerubabele, usataye mtima iwe Yoswa, mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, musataye mtima inu nonse. Yambani ntchito, pakuti Ine ndili nanu ndithu. Musachite mantha, popeza kuti mzimu wanga uli pakati panu, monga momwe ndidalonjezera pamene munkatuluka ku Ejipito. “Zimene ndikunena Ine Chauta Wamphamvuzonse ndi izi: Patapita nthaŵi pang'ono, ndidzagwedeza mlengalenga ndi dziko lapansi, nyanja ndi mtunda. Ndidzagwedeza mitundu yonse ya anthu ndipo chuma cha anthu onse chidzabwera, motero Nyumba imeneyi ndidzaidzaza ndi ulemerero waukulu. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. Siliva yense ndi wanga, golide yense ndi wanga. Choncho ulemerero wa Nyumba yachiŵiriyi udzaposa ulemerero wa Nyumba yoyamba ija. Ndipo ndidzakhazikitsa ufulu ndi mtendere pa malo ano. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.” Chaka chachiŵiri cha ufumu wa Dariusi pa tsiku la 24 la mwezi wachisanu ndi chinai, Chauta adapatsa mneneri Hagai uthenga uwu wakuti, “Zimene ndikunena Ine Chauta Wamphamvuzonse ndi izi: Mupemphe ansembe kuti agamule nkhani iyi: Ngati munthu wakulunga nyama yopatulika mu mkanjo wake, ndipo mkanjowo ukhudza buledi kapena msuzi, kapena vinyo, kapena mafuta, kapena chakudya cha mtundu wina uliwonse, kodi zimenezinso zidzasanduka zopatulika? Ansembewo adayankha kuti, ‘Iyai.’ ” Apo Hagai adaŵafunsanso kuti, “Nanga ngati munthu amene adaipitsidwa pokhudza mtembo, akhudzanso zimenezi, ndiye kuti zimenezinso zidzaipitsidwa?” Ansembe adayankha kuti, “Inde, zidzaipitsidwa.” Hagai adanena kuti, “Zimene akunena Chauta ndi izi: ‘Nchimodzimodzinso ndi anthu ameneŵa, nchimodzimodzinso ndi mtundu umenewu pamaso panga. Zonse zimene amachita ndi zonse zimene amapereka ku nsembe nzoipitsidwa. “ ‘Tsopano muganizire zimene zinkachitika asanayambe kumanganso Nyumba ya Chauta. Pamene munthu ankayembekeza kupeza miyeso ya tirigu makumi aŵiri ankangopeza khumi yokha. Akabwera kuti adzatunge miyeso makumi asanu mu mtsuko wa vinyo, ankangopeza makumi aŵiri okha. Ndidaononga mbeu zanu zonse ndi chinsikwi, chinoni ndi matalala. Komabe simudaganize zolapa,’ akutero Chauta. “Lero ndi tsiku la 24, mwezi wachisanu ndi chinai, tsiku limene maziko a Nyumba ya Chauta aikidwa. Muganizirepo tsono, mulibe chakudya chambiri m'nkhokwe. Mpesa, mkuyu, makangaza ndiponso mtengo wa olivi zikali zosabereka. Koma kuyambira lero ndidzakudalitsani.” Tsiku limenelo, tsiku la 24 la mwezi, Chauta adapatsanso Hagai kachiŵiri uthenga uwu wakuti, “Umuuze Zerubabele bwanamkubwa wa ku Yuda, kuti ndidzagwedeza mlengalenga ndi dziko lapansi. Ndidzagwetsa mafumu a mitundu ya anthu akunja ndi kuwononga mphamvu za maufumu ao. Ndidzagubuduza magaleta ndi okwerapo ake. Akavalo adzafa, ndipo okwerapo ao adzaphana. “Ine Chauta Wamphamvuzonse mau anga ndi aŵa: Pa tsiku limenelo iwe Zerubabele mtumiki wanga, mwana wa Salatiyele, ndidzakutenga ndipo ndidzakusandutsa wolamulira m'dzina langa, pakuti ndiwe amene ndakusankhula. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.” Mwezi wachisanu ndi chitatu, chaka chachiŵiri cha ufumu wa Dariusi, Chauta adapatsa mneneri Zekariya, mwana wa Berekiya, mdzukulu wa Ido, uthenga uwu wakuti, “Chauta adaŵakwiyira kwambiri makolo anu. Tsono uŵauze anthuŵa kuti zimene akunena Chauta Wamphamvuzonse ndi izi, akuti, Bwererani kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu. Musakhale ngati makolo anu, amene adamva mau a aneneri akale ofotokoza uthenga wanga wakuti, ‘Lekani makhalidwe anu oipa ndi ntchito zanu zoipa.’ Koma iwowo sadamve kapena kulabadako, akutero Chauta. Kodi makolo anuwo ali kuti tsopano? Nanga aneneri, kodi amakhalapo mpaka muyaya? Kodi mau anga ndi malamulo anga amene ndidauza atumiki anga aneneri, suja adamveka kwa makolo anu? Choncho iwo adalapa ndi kunena kuti, ‘Chauta Wamphamvuzonse watichitadi zomwe adaatsimikiza kuti adzatichita, potsata makhalidwe athu ndi ntchito zathu zoipa.’ ” Tsiku la 24 la mwezi wa khumi ndi umodzi, mwezi wa Sebati, chaka chachiŵiri cha ufumu wa Dariusi, Chauta adapatsa uthenga mneneri Zekariya, mwana wa Berekiya, mdzukulu wa Ido. Tsono Zekariya adati, “Usiku wathawu ndinaona zinthu m'masomphenya. Ndinaona munthu atakwera pa kavalo wofiira. Munthuyo anaima pa timitengo tazitsamba m'chigwa. Kumbuyo kwake kunalinso akavalo, ena ofiira, ena odera, ena oyera. Ndiye ine ndinamufunsa kuti, ‘Mbuye wanga, kodi nchiyaninso chikatere?’ Mngelo amene ankalankhula nane anayankha kuti, ‘Ndikufotokozera tanthauzo lake.’ Tsono munthu amene anaima pa timitengo tazitsamba uja anayankha kuti, ‘Ameneŵa ndiwo amene Chauta waŵatuma kuti ayendere dziko lapansi.’ Ndipo onsewo anauza mngelo wa Chauta amene anaima pakati pa timitengo tazitsamba uja, kuti, ‘Tayendera dziko lapansi, ndipo anthu onse ali pa mtendere, akupumula.’ Tsono mngelo wa Chautayo anafunsa kuti, ‘Inu Chauta Wamphamvuzonse, kodi Yerusalemu ndi mizinda ya ku Yuda imene mudaikwiyira pa zaka makumi asanu ndi aŵiri, mudzakhalabe oiwumira mtima mpaka liti?’ Chauta anamuyankha mau abwino ndi okondweretsa mngelo amene amalankhula naneyo. Pamenepo mngeloyo anandiwuza kuti, ‘Lengeza kuti, Chauta Wamphamvuzonse akuti, “Maganizo anga onse ndi mtima wanga wonse zili pa Yerusalemu ndi Ziyoni. Ndaŵakwiyira kwambiri anthu a mitundu ina amene ali pa mtendere. Pamene ndinkakwiyira anthu anga motsinira, mpamene anthu enawo ankakakatira kuzunza anthu anga. Nchifukwa chake ndabwerera ku Yerusalemu ndi mtima wachifundo. Nyumba yanga adzaimanganso kumeneko, ndipo adzatenga chingwe choyesera kuti amangenso mzinda wa Yerusalemu,” akutero Chauta Wamphamvuzonse. Ulengezenso kuti Chauta Wamphamvuzonse akuti, “M'mizinda yangayi mudzakhalanso chuma chambiri. Ndidzasangalatsanso Ziyoni, ndipo Yerusalemu ndidzamsandutsanso mzinda wanga wapamtima.” ’ ” “Pambuyo pake m'masomphenyanso ndidaona nyanga zinai. Ndidafunsa mngelo amene ankalankhula nane tanthauzo lake la nyanga zimenezo. Iye adandiyankha kuti, ‘Zimenezi ndizo mphamvu zapansi pano zimene zidabalalitsa anthu a ku Yuda, a ku Israele ndi a ku Yerusalemu.’ “Kenaka Chauta adandiwonetsa amisiri anai osula. Ine ndidafunsa kuti, ‘Kodi akudzachita chiyani?’ Iye adayankha kuti, ‘Mphamvu zijazi zidabalalitsa Yuda ndi Yerusalemu kotheratu, kotero kuti panalibe ndi mmodzi yemwe woŵeramutsa mutu. Koma amisiri osulaŵa, abwera kudzaopsa ndi kudzaononga mphamvu za mitundu ya anthu imene idaagonjetsa dziko la Yuda, ndi kumwaza anthu ake.’ ” Ndidaonanso zinthu m'masomphenya: ndidaona munthu atatenga chingwe choyesera m'manja mwake. Ndidamufunsa kuti, “Kodi mukupita kuti?” Iye adandiyankha kuti, “Ndikukayesa mzinda wa Yerusalemu kuti ndidziŵe kutalika kwa muufupi mwake ndi m'litali mwake.” Apo mngelo uja ankalankhula naneyu adasendera, mngelo winanso adadzakumana naye. Woyamba uja adauza mnzakeyo kuti, “Thamangira mnyamata wachingweyo, ukamuuze kuti mu Yerusalemu mudzakhala anthu ambiri ndiponso zoŵeta zochuluka, kotero kuti mzindawo udzakhala wopanda malinga. Chauta akuti Iye yemwe ndiye adzakhale linga lamoto loteteza mzindawo, ndipo adzaonetsa ulemerero wake m'kati mwake.” Chauta akunena kuti, “Tiyeni, tiyeni, thaŵaniko ku dziko lakumpoto. Paja ndidakumwazirani ku mphepo zinai za mlengalenga. Tiyeni, thaŵirani ku Ziyoni, inu amene mudatengedwa ukapolo kupita ku Babiloni. Aliyense wokantha inu, wakantha chinthu cha mtengo wapatali zedi kwa Ine.” Tsono Chauta Wamphamvuzonse adandituma kwa mitundu imene idaagwira anthu ake kukaiwuza uthenga wake wakuti, “Ine Chauta ndidzaŵamenya anthuwo ndi dzanja langa, ndipo amene anali akapolo ao, ndiwo amene adzaŵalande chuma chao.” Pamenepo mudzadziŵa kuti Chauta Wamphamvuzonse ndiye wandituma. “Inu anthu a ku Ziyoni, imbani mokondwa, chifukwa ndikubwera, ndikudzakhala pakati panu,” akutero Chauta. Nthaŵi imeneyo anthu a mitundu yambiri adzabwera kwa Chauta, adzasanduka anthu ake, ndipo Iye adzakhala pakati panu. Apo mudzadziŵa kuti Chauta Wamphamvuzonse ndiye wandituma kwa inu. Iyeyo adzamtenganso Yuda kuti akhale chuma chake m'dziko lopatulika, ndipo Yerusalemu adzakhala mzinda wake wapamtima. Anthu nonsenu, ingokhalani chete pamaso pa Chauta, chifukwa wadzambatuka ndi kutuluka ku malo ake oyera. Tsono m'masomphenya Chauta adandiwonetsa Yoswa, mkulu wa ansembe, ataima pamaso pa mngelo wake, ku dzanja lake lamanja kutaima Satana woti amuimbe mlandu. Mngelo wa Chauta uja adauza Satanayo kuti, “Chauta akudzudzule, iwe Satana! Chauta amene adasankhula Yerusalemu akudzudzule ndithu iwe! Kodi uyu sali ngati chikuni choyaka chofumula pa moto?” Yoswa anali atavala zovala zalitsiro, pa nthaŵi imene adaaima pamaso pa mngelo uja. Tsono mngeloyo adauza anzake omperekeza kuti, “Mvuleni zovala zake zalitsirozi.” Kenaka adauza Yoswa kuti, “Ona ndakuchotsera machimo ako, tsopano ndikuveka zovala zokongola.” Mngelo uja adauza omperekeza aja kuti, “Mvekeni nduŵira yabwino.” Motero adamuveka nduŵira yabwino pa mutu, namuvekanso zovala zatsopano. Nthaŵiyo nkuti mngelo wa Chautayo ataima pomwepo. Mngelo wa Chauta uja adauza Yoswa kuti, “Zimene akunena Chauta Wamphamvuzonse ndi izi, akuti, ‘Mukamayenda m'njira yanga, ndi kumamveradi malamulo anga, mudzalamulira m'nyumba mwanga, ndipo mudzayang'anira mabwalo anga. Tsono ndidzakulolani kuti mudzakhale pamodzi ndi aŵa ali panoŵa. Tsopano imva, iwe Yoswa, mkulu wa ansembe, imvani nanunso ansembe anzakenu, amene muli chizindikiro cha zabwino zimene zidzachitike. Ndidzabwera naye mtumiki wanga wotchedwa dzina loti “Nthambi.” Nawutu mwala umene ndaika pamaso pa Yoswa, mwala umodzi wa mbali zisanu ndi ziŵiri. Mwiniwakene ndidzazokotapo mau, ndidzachotsa machimo a m'dziko lino pa tsiku limodzi. Tsiku limenelo, nonsenu mudzaitanizana kuti mukakondwerere ufulu wanu, aliyense atakhala pa mtengo wake wa mphesa ndi wa mkuyu,’ akutero Chauta Wamphamvuzonse.” Pambuyo pake mngelo amene ankalankhula nane uja adabweranso nandidzutsa monga momwe amadzutsira munthu amene ali m'tulo. Adandifunsa kuti, “Ukuwona chiyani?” Ine ndidayankha kuti, “Ndikuwona choikaponyale, chonse chagolide, ndi mbale pamwamba pake. Chili ndi nyale zisanu ndi ziŵiri, iliyonse ili ndi ziboo zisanu ndi ziŵiri zoloŵetsamo zingwe zoyatsira. Pambali pake pa choikaponyalecho pali mitengo iŵiri ya olivi, wina ku dzanja lamanja, wina ku dzanja lamanzere.” Ndiye mngelo amene anali naneyo ndidamufunsa kuti “Mbuye wanga, kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?” Mngeloyo adayankha kuti, “Monga iwe zimenezi sukuzidziŵa?” Ine ndidati, “Inde, mbuye wanga, sindikuzidziŵa.” Tsono iye adandiwuza kuti ndidziŵitse Zerubabele uthenga wa Chauta wakuti, “Inde udzapambana, koma osati ndi nkhondo kapena ndi mphamvu, koma ndi mzimu wanga. Kodi iwe phiri lalitali, ndiwenso chiyani? Udzasanduka dziko losalala pamaso pa Zerubabele. Ndipo akadzabwera nawo mwala wotsiriza wa pa Nyumba yanga, namauika pamwamba, anthu adzafuula kuti, ‘Ati kukongola ati!’ ” Chauta adandipatsanso uthenga uwu wakuti, “Zerubabele adamanga maziko a nyumba imeneyi ndi manja ake, adzaitsiriza ndi manja ake omwewo. Motero anthu adzadziŵa kuti Chauta Wamphamvuzonse adandituma kwa iwo. Pakali pano anthuwo ndi okhumudwa kuwona kuti ntchito sikufulumira. Koma akadzamuwona Zerubabele atatenga mwala wotsiriza uja m'manja mwake, pamenepo adzakondwa. “Nyale zisanu ndi ziŵiri ndi maso a Chauta amene akunka nayang'anayang'ana pa dziko lonse lapansi.” Tsono ndidamufunsa munthuyo kuti, “Nanga mitengo iŵiri ya olivi ili kumanja ndi kumanzere kwa choikaponyalecho ikutanthauza chiyani?” Ndidamufunsanso kuti, “Pambali pa mipopi iŵiri yagolide yodzera mafutayo pali nthambi ziŵiri za mtengo wa olivi, zimenezi zikutanthauza chiyani?” Iye adati, “Monga iwe zimenezi sukuzidziŵa?” Ine ndidayankha kuti, “Inde, mbuye wanga, sindikuzidziŵa.” Tsono iye adati, “Ameneŵa ndi anthu aŵiri odzozedwa aja, amene amatumikira Chauta, Ambuye a dziko lonse lapansi.” Ndidaonanso zinthu zina m'masomphenya: ndidaona chikalata chofutukula chikuuluka. Mngelo uja adandifunsa kuti “Kodi ukuwona chiyani?” Ine ndidayankha kuti, “Chikalata chofutukula chikuuluka, muutali mwake mamita asanu ndi anai, muufupi mwake mamita anai ndi hafu.” Tsono adandiwuza kuti, “Pamenepo palembedwa temberero limene lidzagwera dziko lonse lapansi. Aliyense wakuba adzachotsedwa m'dziko potsata zimene zalembedwa mbali iyi, ndipo aliyense wolumbira zabodza nayenso adzachotsedwa potsata zimene zalembedwa mbali inai. Chauta Wamphamvuzonse wanena kuti, ‘Temberero limeneli ndidzalitumiza m'nyumba ya munthu wakuba ndi m'nyumba ya munthu wolumbira zabodza potchula dzina langa. Lidzakhala m'nyumbamo mpaka kuiwonongeratu, mitengo yake ndi miyala yake yomwe.’ ” Pambuyo pake mngelo amene ankalankhula nane uja adabwera, nandiwuza kuti, “Upenyetsetse, uwone chinthu chikubwerachi.” Ndidafunsa kuti, “Kodi nchiyani?” Iye adati, “Chimenechi ndi gondolo loyesera, ndipo likutanthauza uchimo wa anthu m'dziko lonse.” Chovundikira chake chinali chamtovu, ndipo chitatukuka, ndidaona mkazi atakhala tsonga m'gondolomo. Mngeloyo adati, “Ameneyu akutanthauza kuipa konse.” Atatero adakankhira mkaziyo m'gondolo muja, nabwezera chovundikira chamtovu chija pamwamba pake. Nditayang'ananso, ndidaona akazi aŵiri okhala ndi mapiko onga a kakoŵa. Akaziwo ankabwera chouluka ndi mphepo. Adanyamula gondolo lija, kupita nalo pakati pa dziko lapansi ndi mlengalenga. Tsono ndidafunsa mngelo amene ankalankhula nane kuti, “Nanganso gondololi akupita nalo kuti?” Iye adandiyankha kuti, “Akupita nalo ku dziko la Sinara kuti akalimangire nyumba. Nyumbayo ikadzatha, adzakhazikamo gondololo pa phaka lake.” Pambuyo pake ndidaona zinthu zinanso m'masomphenya: ndidaona magaleta anai akutuluka pakati pa mapiri aŵiri, mapiri ake amkuŵa. Galeta loyamba linkakokedwa ndi akavalo ofiira, lachiŵiri akavalo akuda, lachitatu akavalo oyera, lachinai linkakokedwa ndi akavalo otuŵa a maŵanga ofiirira. Tsono ndidafunsa mngelo amene ndinkalankhula naye uja kuti, “Mbuye wanga, kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?” Iye adayankha kuti, “Zimenezi zikutanthauza mphepo zinai zakumwamba, zimene zimachokera kwa Chauta, Ambuye a dziko lonse lapansi. Galeta la akavalo akudali likupita ku dziko lakumpoto. Galeta la akavalo oyerali likupita kutali kuzambwe. Galeta la akavalo amaŵangali likupita ku dziko lakumwera, ndipo galeta la akavalo ofiirali likupita ku dziko lakuvuma.” Akavalowo atatuluka, anali ndi phamphu kufuna kuyendera dziko lonse lapansi. Iye uja adaŵauza kuti, “Pitani mukayendere dziko lapansi.” Akavalowo adapitadi kukayendera dziko lapansi. Apo mngeloyo adandiŵuza mokweza mau kuti, “Amene apita ku dziko lakumpotowo atsitsa mzimu wanga kumeneko.” Kenaka Chauta adandipatsa uthenga wakuti, “Ulandire mphatso kwa anthu aŵa: Heledai, Tobiya, ndi Yedaya, amene abwerako ku ukapolo wa ku Babiloni. Iweyo upite tsiku lomwelo kwa Yosiya mwana wa Zefaniya. Siliva ndi golide amene ulandireyo upangire chisoti chaufumu. Chisoticho uchiike pamutu pa mkulu wa ansembe uja Yoswa, mwana wa Yehozadaki. Tsono umuuze kuti, Zimene ndikunena Ine Chauta Wamphamvuzonse ndi izi: Ndi ameneyutu munthu wotchedwa ‘Nthambi’ uja. Adzaphuka ndi kukulira pomwe aliripo, ndipo adzamangapo Nyumba ya Chauta. Ndiye amene adzamange Nyumba ya Chauta. Ndiye amene adzakhale ndi ukulu waufumu, ndi kumalamulira atakhala pa mpando wake waufumu. Pafupi ndi mpando wake padzakhala wansembe, ndipo aŵiriwo adzagwira ntchito mwamtendere ndi mogwirizana. Chisoti chaufumucho azidzachisunga m'Nyumba ya Chauta, kuti chikhale chikumbutso kwa Heledai, Tobiya, Yedaya ndi Yosiya, mwana wa Zefaniya. “Anthu okhala kutali adzabwera kudzamanga Nyumba ya Chauta. Motero mudzadziŵa kuti Chauta Wamphamvuzonse wandituma kwa inu. Zimenezi zidzachitika ngati mumveradi mwachangu Chauta, Mulungu wanu.” Pa chaka chachinai cha ufumu wa Dariusi, tsiku lachinai la Kisilevi, mwezi wachisanu ndi chinai, Chauta adapatsa Zekariya uthenga. Anthu a ku Betele anali atatuma Sarezere ndi Regemumeleki ndi anthu ao, kuti akapemphe chifundo kwa Chauta. Kwinanso adaati akafunse ansembe a ku Nyumba ya Chauta Wamphamvuzonse ndiponso aneneri kuti, “Kodi ifeyo tizilira ndi kusala chakudya pa mwezi wachisanu monga m'mene takhala tikuchitira pa zaka zambiri?” Tsono Chauta Wamphamvuzonse adandipatsa uthenga uwu wakuti: “Funsa anthu onse a m'dziko ndi ansembe kuti, ‘Pamene munkasala zakudya ndi kulira pa mwezi wachisanu ndi pa mwezi wachisanu ndi chiŵiri zaka makumi asanu ndi aŵiri zapitazi, kodi munkalemekezadi Ine pochita zimenezo? Kodi pamene munkadya ndi kumwa, suja munkangodzikondweretsa nokha? Pajatu nzimenezi zija ankanena Chautazi kudzera mwa aneneri akale, pamene munali modzaza ndi anthu ndiponso zinthu zinkapita m'tsogolo mu mzinda wa Yerusalemu ndi m'mizinda yake yozungulira, ku madera a kumwera ndi ku chigwa.’ ” Chauta adapatsa Zekariya uthenga uwu wakuti, “Zimene ndikunena Ine Chauta Wamphamvuzonse ndi izi: Muziweruzana molungama. Muzimverana chisoni ndi kuchitirana chifundo. Musamazunze akazi amasiye ndi ana amasiye, alendo ndiponso amphaŵi. Musamaganizirane zachiwembu m'mitima mwanu. “Koma iwowo adakana kumvera, adandifulatira ndi mtima wokanika. Adatseka makutu ao kuti asamve. Mitima yao adaiwumitsa kwambiri, kuti asamve malamulo ndi mau amene Ine Chauta Wamphamvuzonse ndidaŵaphunzitsa ndi Mzimu wanga kudzera mwa aneneri amakedzana. Nchifukwa chake Ine Chauta Wamphamvuzonse ndidaŵakwiyira kwambiri. Poti sadandimvere nditaŵaitana, Inenso sindidaŵamvere atandiitana. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. Monga momwe amachitira kamvulumvulu, ndidaŵamwaza pakati pa mitundu ina ya anthu imene iwo sankaidziŵa, ndipo dziko lao lidasanduka chipululu, kotero kuti palibenso wina amene ankayendamo. Choncho dziko lao lokomalo lidasandukadi chipululu.” Chauta Wamphamvuzonse adandipatsanso uthenga uwu wakuti, “Zimene ndikunena Ine Chauta Wamphamvuzonse ndi izi: Mtima wanga wonse uli pa Ziyoni, anthu ake ndimaŵakonda mwansanje kwambiri. Ine Chauta Wamphamvuzonse mau anga ndi aŵa: Tsopano ndidzabweranso ku phiri la Ziyoni, ndidzakhalanso ku Yerusalemu. Yerusalemuyo adzatchedwa Mzinda Wokhulupirika. Phiri la Ine Chauta Wamphamvuzonse lidzatchedwa Phiri Loyera. “Ine Chauta Wamphamvuzonse ndikunena kuti, amuna ndi akazi okalamba, oyenda ndi ndodo chifukwa cha ukalamba, adzayendanso m'miseu ya Yerusalemu. Ndipo m'miseu ya mumzindamo mudzadzaza ndi ana, anyamata ndi atsikana, amene azidzaseŵeramo. “Ine Chauta Wamphamvuzonse mau anga ndi aŵa: Ngakhale ziwoneke ngati zosatheka kwa anthu a m'fuko limeneli amene adzatsale nthaŵi imeneyo, kodi zimenezi zidzakhalanso zosatheka ndi kwa Ine ndemwe? “Ine Chauta Wamphamvuzonse ndikunena kuti, Ndidzapulumutsa anthu anga amene ali ku maiko akuvuma ndi akuzambwe. Ndidzaŵabweza kuti akhalenso ku Yerusalemu. Pamenepo adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao, wokhulupirika ndi wolungama. “Zimene ndikunena Ine Chauta Wamphamvuzonse ndi izi: Inu masiku ano mukumva mau a aneneri amene ankalankhula pa nthaŵi yoyala maziko a Nyumba ya Chauta Wamphamvuzonse. Choncho limbani mtima, kuti Nyumbayi imangidwenso. Mpaka nthaŵi imeneyo panalibe wina wolandirapo malipiro pa ntchito kapena wopindulapo pa zoŵeta. Panalibe munthu amene ankadziyendera mwamtendere, chifukwa cha adani, popeza kuti anthu onse ndidaaŵayambanitsa. Koma tsopano anthu atsalaŵa sindidzaŵachitanso zomwe ndidaaŵachita anthu kale. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. “Adzabzala mwamtendere, mpesa udzabala zipatso zake, ndipo nthaka idzabereka kwambiri. Mvula idzagwa kuchokera kumwamba. Madalitso onseŵa ndidzaŵapatsa otsala mwa anthuŵa. Inu mabanja a Yuda ndi Israele, kale munali chizindikiro cha matemberero pakati pa mitundu ina ya anthu. Koma tsopano ndidzakupulumutsani ndipo mudzakhala chizindikiro cha madalitso. Musaope, limbani mtima. “Ine Chauta Wamphamvuzonse mau anga ndi aŵa: Paja ndidaatsimikiza mtima kuti ndikuwonongeni, chifukwa chakuti makolo anu adaandikwiyitsa, ndipo sindidafune kukhululuka. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. Koma masiku ano ndatsimikiza kuti ndimchitira zabwino Yerusalemu ndi banja la Yuda. Choncho musaope. Muzichita izi: muzikambirana zoona, muziweruza moona ndi mwamtendere m'mabwalo a milandu. Musamachitirane chiwembu, musamakonde kulumbira zonama, pakuti zonsezi ndimadana nazo.” Ndikutero Ine Chauta. Chauta Wamphamvuzonse adandipatsa uthenga uwu wakuti, “Ine Chauta Wamphamvuzonse mau anga ndi aŵa: Kusala zakudya pa mwezi wachinai, wachisanu, wachisanu ndi chiŵiri ndi wakhumi, kudzakhala nthaŵi yachimwemwe ndi yachisangalalo ku banja la Yuda. Muzikonda zoona ndiponso mtendere.” “Zimene ndikunena Ine Chauta Wamphamvuzonse ndi izi: Anthu a mitundu yambiri ndi anthu okhala m'mizinda yambiri adzabweradi. Anthu a mzinda wina adzapita ku mzinda wina, kukanena kuti, ‘Tiyeni mwamsanga tikapemphe chifundo kwa Chauta, tikapembedze Chauta Wamphamvuzonse. Ifeyo tikupita komweko.’ Anthu ambiri ndiponso a ku maiko amphamvu adzandipembedzadi Ine Chauta Wamphamvuzonse ku Yerusalemu ndi kupempha chifundo changa. “Ine Chauta Wamphamvuzonse ndikunena kuti, pa masiku amenewo anthu khumi ochokera ku mitundu ya anthu a zilankhulo zosiyana adzagwira mkanjo wa Myuda ndi kunena kuti, ‘Tipite nao, chifukwa tamva kuti Mulungu ali nanu.’ ” Mau a Chauta akudzudzula dziko la Hadaraki, ndiponso mzinda wa Damasiko. Paja mizinda yonse ya ku Aramu njake ya Chauta, chimodzimodzi ngati mafuko onse a Aisraele. Ndi wa Chautanso mzinda wa Hamati, umene ukuchitana malire ndi maikowo, chimodzimodzinso Tiro ndi Sidoni ngakhale ndi anzeru kwambiri. Tiro adadzimangira linga. Adaunjika siliva ngati dothi, adakundika golide ngati chifwilimbwiti cham'miseu. Koma taimani, Chauta adzamlanda chuma chonsechi, adzachitaya m'nyanja, iyeyo adzapserera ndi moto. Mzinda wa Asikeloni nawonso udzaziwona zimenezo, nkuchita mantha. Gaza adzakhwinyata ndi mantha, Ekeroninso chimodzimodzi, chifukwa zimene ankayembekeza zidzasokonezeka. Mfumu ya ku Gaza idzachotsedwa, ku Asikeloni kudzakhala kopanda anthu. Ku Asidodi kudzakhala anthu achimsakaniza. Chauta akuti, “Ndidzathetsa kunyada kwa Filistiya. Anthu ake sadzadyanso nyama yamagazi, kapena nyama yoletsedwa iliyonse. Otsala onse adzakhala anthu anga, adzasanduka ngati fuko la ku Yuda. Nawonso Aekeroni adzakhala ngati Ayebusi. Pamenepo Ine ndidzakhala mlonda wa dziko langalo, kuti wina asamadutsepo kapena kuloŵamo. Palibe adani amene adzaŵapambane, pakuti zimenezi ndikuzisamala Ine ndemwe.” Kondwani kwambiri, inu anthu a ku Ziyoni. Fuulani kwambiri, inu anthu a ku Yerusalemu. Onani, mfumu yanu ikudza kwa inu. Ikubwera ili yopambana ndi yogonjetsa adani. Ndi yodzichepetsa ndipo yakwera pa bulu, bulu wake kamwana tsono. Ndidzachotsa magaleta ankhondo ku Efuremu ndi akavalo ankhondo ku Yerusalemu. Uta wankhondo adzauthyola. Mfumu yanu idzachititsa mtendere pakati pa mitundu yonse ya anthu. Adzalamulira kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja ina, ndiponso kuchokera ku Mtsinje wa Yufurate mpaka ku mathero a dziko lapansi. Chauta akuti, “Tsono kunena za inu, chifukwa cha chipangano changa ndi inu, chimene nsembe zamagazi zidachitsimikiza, ndidzaŵatulutsa m'dzenje lopanda madzi anthu anu amene ali ngati akapolo. Bwererani ku linga lanu lolimba, inu akapolo amene tsopano muli ndi chikhulupiriro. Lero ndi tsiku limene ndikulengeza kuti ndidzakubwezerani zabwino moŵirikiza. “Ndidzakoka Yuda ngati uta wanga, Efuremu adzakhala ngati muvi wake. Ndidzatenga ana ako, iwe Ziyoni, kuti alimbane ndi ana ako, iwe Grisi; ndidzakugwira ngati lupanga la wankhondo wamphamvu.” Tsono Chauta adzaonekera anthu ake, ndipo mivi yake adzaiponya ngati zing'aning'ani. Ambuye Chauta adzaliza lipenga, ndipo adzayenda m'kamvulumvulu wochokera kumwera. Chauta Wamphamvuzonse adzakhala chishango chao. Iwowo adzapambana ndi kugonjetsa adani ao poponya miyala chabe. Adzamwa magazi ao nkumafuula ngati okhuta vinyo. Magaziwo adzachita kuyenderera ngati magazi a nsembe, othira ndi mkhate pa guwa popembedza. Tsiku limenelo Chauta, Mulungu wao, adzaŵapulumutsa, pakuti anthu akewo ali ngati nkhosa. M'dziko laolo anthuwo adzakhala onyezimira ngati miyala ya mtengo wapatali ya pa chisoti chaufumu. Dzikolo lidzakhaladi lokongola kwambiri. Tirigu adzalimbitsa anyamata, ndipo vinyo watsopano adzakometsa anamwali. Pemphani Chauta kuti akupatseni mvula pa nyengo yobzala. Ndiye amene amapanga mitambo yamvula. Ndiye amene amagwetsera anthu mvula yamvumbi, ndiye amene amameretsera aliyense mbeu m'munda. Paja mafano am'nyumba amalankhula zonama, ndipo oombeza maula amaona zabodza. Olota maloto amalota zabodza, ndipo mau ao othuzitsa mtima ndi nkhambakamwa chabe. Motero anthu amangoyenda uku ndi uku ngati nkhosa, amazunzika chifukwa chosoŵa mbusa. Chauta akuti, “Ndaŵakwiyira kwambiri abusa, ndipo atsogoleri a m'dzikomo ndidzaŵalanga. Koma Ine Chauta Wamphamvuzonse ndidzasamala nkhosa zanga, ndiye kuti banja la Yuda, ndipo ndidzazisandutsa ngati akavalo ankhondo amphamvu. Mwa iwo mudzatuluka mtsogoleri amene adzakhala ngati mwala wapangodya, ngati uta wankhondo. Ndipo atsogoleri onse olamulira adzachokeranso mwa iyeyo. Ayuda onse pamodzi adzakhala ngati ngwazi zankhondo, zopondereza adani m'matope am'miseu nthaŵi yankhondo. Adzamenya nkhondo chifukwa choti Chauta ali nawo, ndipo adzagonjetsa adani okwera pa akavalo. “Banja la Yuda ndidzalilimbitsa, banja la Yosefe ndidzalipambanitsa. Anthuwo ndidzaŵabwezanso kwao chifukwa choti ndaŵamvera chifundo. Tsono adzakhala ngati kuti sindidaŵataye, pakuti Ine ndine Chauta, Mulungu wao, ndipo ndidzayankha zopempha zao. Pamenepo Aefuremu adzakhala ngati ankhondo amphamvu, adzasangalala ngati anthu okhuta vinyo. Ana ao adzaziwona zimenezi, nawonso nkusangalala, mumtima mwao mudzadzaza chimwemwe, chifukwa cha zimene Chauta wachita. “Ndidzaliza mluzu kuti anthu anga asonkhane pamodzi. Ndidaŵapulumutsa, ndipo adzachuluka monga momwe adaaliri masiku amakedzana. Ngakhale ndidaŵabalalitsira pakati pa mitundu ya anthu, komabe ku maiko akutaliwo adzandikumbukira. Iwowo pamodzi ndi ana ao adzakhala moyo nadzabwerera. Ndidzaŵatulutsa ku Ejipito ndi kupita nawo kwao, ndipo ndidzaŵasonkhanitsa kuchokera ku Asiriya. Ndidzaŵafikitsa ku dziko la Giliyadi ndi la Lebanoni mpaka kudzaza dziko lonse. Pamene azidzaoloka nyanja ya ku Ejipito, ndidzathetsa mafunde a pa nyanjayo, madzi onse a mtsinje wa Nailo adzaphweratu. Kudzikuza kwa Asiriya kudzatha, ndipo ndodo yaufumu ya Ejipito idzathyoka. Ineyo ndidzalimbitsa anthu anga, ndipo adzakhala onyadira dzina la Chauta.” Ndikutero Ine Chauta. Tsekula zitseko zako, iwe Lebanoni, kuti moto upsereze mikungudza yako. Lirani mokweza, inu mitengo ya paini, pakuti mikungudza yagwa, mitengo yamphamvu yaonongeka. Lirani mokweza inu mitengo ya thundu ya ku Basani, pakuti nkhalango yoŵirira ija aiyeretsa. Imvani abusa, nawonso akulira mokweza, pakuti mabusa ao obiriŵira auma. Imvani misona ya mikango ikubangula, pakuti nkhalango yoŵirira ya ku Yordani aiyeretsa. Chauta, Mulungu wanga, adandiwuza kuti, “Ŵeta bwino nkhosa zimene zili kukaphedwa. Amene amagula nkhosa amazipha, koma salangidwa. Amene amazigulitsa amanena kuti, ‘Atamandike Chauta, ine ndalemera!’ Ndipo abusa ake sadzazimvera chifundo nkhosazo. Choncho onse okhala m'dziko lapansi, sindidzaŵamveranso chifundo. Ndikutero Ine Chauta. Munthu aliyense ndidzampereka m'manja mwa mtsogoleri wake ndi mwa mfumu yake. Ndipo iwowo adzasakaza dziko lonse, koma Ine sindidzampulumutsa aliyense m'manja mwao.” Tsono ine ndidayamba kuŵeta nkhosa zokaphedwa zija. Ndidatenga ndodo ziŵiri: yoyamba ndidaitcha dzina lakuti “Kukoma mtima”, yachiŵiri ndidaitcha “Umodzi.” Tsono gulu la nkhosa lija ndidaliŵetadi bwino. Pa mwezi umodzi ndidachotsa abusa atatu aja. Adafika pondipsetsa mtima, ine osathanso kuŵapirira. Iwonso adadana nane. Tsono ndidauza gulu la nkhosa lija kuti, “Sindidzakuŵetaninso. Imene ikuti ife, ife basi. Imene ikuti isokere, isokere, ndipo otsalanu, muzidyana.” Pambuyo pake ndidatenga ndodo yanga ija yotchedwa “Kukoma mtima” ndi kuithyola, kusonyeza kuphwanya chipangano chimene ndidaapangana ndi mitundu yonse ya anthu. Motero chipanganocho chidatha tsiku limenelo, ndipo ochita malonda a nkhosa aja, amene ankangondiyang'anitsitsa, adazindikira kuti zonse zimene ndinkachita zinali zochokera kwa Chauta. Tsono eni nkhosawo ndidaŵauza kuti “Ngati zakukomerani, mundilipire. Koma ngati si choncho, sungani ndalama zanu.” Ndiye iwowo adandilipira masekeli asiliva makumi atatu. Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Uziponye mosungira chuma.” Motero ndidatenga masekeli asiliva zija, mtengo uja adaati ndiyenera kulandirawu, nkukaziponya mosungira chuma m'Nyumba ya Chauta. Kenaka ndidathyolanso ndodo ina ija yotchedwa “Umodzi,” kusonyeza kuthetsa ubale pakati pa Yuda ndi Israele. Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Tenganso zida za mbusa, mbusa wake wopandapake. Pakuti ndidzakuika mbusa m'dziko, mbusa amene sadzasamala nkhosa zotayika, sadzanka nafunafuna zosokera, kapena kuchiritsa zopunduka, ndi kudyetsa zamoyo. Koma iye azidzangodya nyama ya nkhosa zonona, mpaka kumapulula ndi ziboda zake zomwe. “Tsoka kwa mbusa wanga wopandapakeyo, amene amasiya nkhosa! Amkanthe ndi lupanga pa mkono, ndi pa diso lake lakumanja. Mkono wakewo ufwape, ndipo diso lakelo lichite khungu kotheratu!” Mau a Chauta onena za Israele. Chauta ndiye adayala mlengalenga ndi kukhazikitsa dziko lapansi, ndiyenso amene adalenga mpweya wokhala mwa munthu. Iye akunena kuti, “Ndidzasandutsa Yerusalemu kuti akhale ngati chikho cha vinyo amene adzasokoneza mitundu yonse ya anthu yomzungulira. Adani omwewo adzathira nkhondo dziko la Yuda ndiponso mzinda wa Yerusalemu. Tsiku limenelo Yerusalemu ndidzamsandutsa mwala wolemera kwambiri kwa mitundu yonse ya anthu. Onse oyesa kuunyamula, udzaŵapweteka koopsa. Mitundu yonse ya anthu a pansi pano idzasonkhana pamodzi kuti imuukire Yerusalemu.” Chauta akunena kuti, “Tsiku limenelo kavalo aliyense ndidzamchititsa mantha osokonezeka nawo, ndipo wokwerapo wake adzachita msala. Banja la Yuda ndidzaliyang'anira, koma akavalo a adani ao onse ndidzaŵachititsa khungu. Pamenepo atsogoleri a Yuda adzavomera kuti, ‘Indedi, anthu a ku Yerusalemu amapeza mphamvu mwa Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wao.’ ” Tsiku limenelo mafuko a ku Yuda ndidzaŵasandutsa ngati mbaula yotentha pakati pa nkhuni, ngati nsakali yoyaka pakati pa mitolo ya tirigu. Adzatentha mitundu yonse ya anthu yoŵazungulira, kumanja ndi kumanzere, koma anthu a ku Yerusalemu adzakhalabe mwamtendere mumzinda mwao. “Chauta adzayamba wapulumutsa mahema onse a ku Yuda, kuti ulemerero wonse wa banja la Davide ndi wa anthu a ku Yerusalemu usapambane ulemerero wa Yuda. Tsiku limenelo Chauta adzakhala ngati chishango chotchinjiriza anthu a ku Yerusalemu, kotero kuti anthu ofooka kwambiri mwa iwo adzakhala amphamvu ngati mfumu Davide. Tsono banja la Davide lidzakhala lolamulira zonse ngati Mulungu, ngati mngelo wa Chauta woŵatsogolera. Tsiku limenelo ndidzaononga mitundu yonse ya anthu yofuna kuthira nkhondo Yerusalemu. “Tsono anthu a pa banja la Davide ndi anthu onse a ku Yerusalemu ndidzaŵadzaza ndi mtima wachifundo ndi wakupemphera. Motero adzati atamuyang'ana amene adambaya, adzamlira kwabasi monga muja amamlirira mwana akakhala mmodzi yekha. Adzamliradi kwambiri monga muja amamlirira mwana wachisambamu. Tsiku limenelo kulira maliro ku Yerusalemu kudzakula monga m'mene kunaliri polira Hadadirimoni m'chigwa cha ku Megido. Dziko lidzalira, banja lililonse palokha. Banja la Davide lidzalira palokha, akazi akenso adzalira paokha. Banja la Natani lidzalira palokha, akazi akenso adzalira paokha. Banja la Levi lidzalira palokha, akazi akenso adzalira paokha. Banja la Simei lidzalira palokha, akazi akenso adzalira paokha. Mabanja onse otsala adzalira paokha, ndipo akazi aonso adzalira paokha.” Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Tsiku limenelo banja la Davide adzalikonzera kasupe wa madzi, kuti iwo pamodzi ndi anthu a ku Yerusalemu aŵachotsere machimo ao ndi zoipa zao. “Tsiku limenelo ndidzafafaniziratu ndi maina omwe a mafano m'dziko, kotero kuti sadzaŵakumbukiranso. Ndidzachotsanso m'dziko aneneri pamodzi ndi mzimu wonyansa Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. Wina aliyense akadzafunabe kuti azilosa, bambo wake ndi mai wake adzamuuza kuti, ‘Sudzakhalanso ndi moyo chifukwa choti ukulosa zabodza m'dzina la Chauta.’ Motero makolo ake omwe adzambaya pamene munthuyo akulosa. “Tsiku limenelo mneneri aliyense adzachita manyazi chifukwa cha zinthu zimene akuti amaziwona m'masomphenya pamene akulosa. Sadzavalanso mwinjiro wake waubweya woti azinamizira anthu. Koma adzati, ‘Sindine mneneri ai. Ndine mlimi, poti ndakhala ndikulima munda kuyambira ubwana wanga.’ Ndipo wina akadzafunsa kuti, ‘Nanga zilonda zili kumsana kwakozi, udatani?’ Iye adzati, ‘Zilondazi ndidazilandira m'nyumba mwa abwenzi anga.’ ” Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Lupanga iwe, dzambatuka, ukanthe mbusa wanga. Ukanthe munthu amene ali pafupi ndi Ine. Ndikutero Chauta Wamphamvuzonse. Kantha mbusa kuti nkhosa zimwazikane. Pamenepo ndidzakantha ndi anthu wamba omwe.” Chauta Wamphamvuzonse akuti, “Mwa zigawo zitatu za anthu m'dziko monsemo ziŵiri zidzaphedwa, chidzangokhalako chigawo chimodzi chokha chamoyo. Anthu a m'chigawo chachitatuchi ndidzaŵaika pa moto, ndidzaŵayeretsa monga m'mene amayeretsera siliva. Ndidzaŵayesa monga m'mene amayesera golide. Tsono adzatama dzina langa mopemba, Ine mwiniwake nkuŵayankha. Ndidzanena kuti, ‘Ameneŵa ndi anthu anga.’ Iwowo adzati, ‘Chauta ndi Mulungu wathu.’ ” Onani, tsiku likubwera, la Chauta, pamene zinthu zomwe adani ako adakulanda, azidzagaŵana iwe uli pomwepo. Chauta adzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse kuti adzathire nkhondo Yerusalemu. Adzaulanda mzindawo ndi kuphwasula nyumba zonse, ndipo akazi am'menemo adzaŵachita chigololo. Theka la anthu a mu mzindawo lidzatengedwa ukapolo, koma ena onse otsala mumzindamo sadzachotsedwa. Pambuyo pake Chauta adzabwera kudzamenyana ndi adani amenewo, monga m'mene amachitira pa tsiku la nkhondo. Tsiku limenelo adzaimirira pa phiri la Olivi loyang'anana ndi Yerusalemu chakuvuma, ndipo phirilo lidzagaŵika paŵiri ndi chigwa chachikulu choyenda kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe. Theka la phiri lidzasunthira chakumpoto, theka lina chakumwera. Inu mudzapulumuka podzera m'chigwa chimenecho cha pakati pa mapiri. Mudzathaŵa monga m'mene mudaathaŵira nthaŵi ija ya chivomezi pa nthaŵi ya Uziya mfumu ya ku Yuda. Kenaka Chauta, Mulungu wanu, adzabwera pamodzi ndi oyera ake onse. Tsiku limenelo sikudzatentha, sikudzazizira ndipo sikudzachita chisanu chambee. Lidzakhala tsiku la kuŵala kokhakokha, osakhala usana, osakhala usiku, chifukwa ndi madzulo omwe kuzidzaŵalabe. Tsiku limene zidzachitike zimenezi ndi Chauta yekha akulidziŵa. Tsiku limenelo madzi a moyo adzatuluka ku Yerusalemu. Theka la madziwo lidzathira m'nyanja yakuvuma, theka lina lidzathira m'nyanja yakuzambwe. Zimenezi zidzachitika pa nthaŵi yachilimwe ndi yachisanu yomwe. Tsono Chauta adzakhala mfumu ya dziko lonse lapansi. Tsiku limenelo Chauta yekha anthu onse adzampembedza, adzamdziŵa ndi dzina lake limodzi lokhalo. Dziko lonse adzalisalaza kuyambira ku Geba mpaka ku Rimoni, kumwera kwa Yerusalemu. Koma Yerusalemu adzakwezedwa pamalo pakepo, kuyambira ku chipata cha Benjamini mpaka ku malo amene kunali chipata chakale mpaka ku chipata chapangodya, ndiponso kuchokera ku Nsanja ya Hananele mpaka ku malo opondera mphesa za mfumu. Anthu adzakhala ku Yerusalemu mwamtendere, poti sadzaopsezedwanso ndi chiwonongeko kumeneko. Pambuyo pake Chauta adzalanga ndi mliri adani onse amene ankamenyana nkhondo ndi Yerusalemu. Matenda ake adzakhala motere: matupi ao adzaola eni ake akuyendabe, maso ao adzaola ali chikhalire m'malo mwake, ndipo malilime ao adzaola m'kamwa mwao. Pa tsiku limenelo Chauta adzasokoneza anthu ndi mantha aakulu, mpaka aliyense adzagwira dzanja la mnzake, ndipo adzayamba kumenyana okhaokha. Nawonso anthu a ku Yuda adzachita nkhondo ku Yerusalemu. Ndipo chuma cha anthu a mitundu yozungulira adzachisonkhanitsa pamodzi. Chuma chake ndi golide ndi siliva wambiri ndiponso zovala zochuluka. Mliri uja udzaphanso akavalo, ngamira ndi abulu a mitundu yonse, ndiponso nyama zonse zokhala ku zithando zankhondo. Zitatha zimenezi anthu onse otsala mwa adani amene ankamenyana ndi Yerusalemu, azidzabwera chaka ndi chaka kudzapembedza Mfumu, Chauta Wamphamvuzonse, ndiponso kudzachita chikondwerero chamisasa. Ngati mabanja ena pa dziko lapansi sadzapita ku Yerusalemu kukapembedza Mfumu, Chauta Wamphamvuzonse, mvula sidzaŵagwera. Ngati anthu a ku Ejipito sadzapita kukaonekera kumeneko, adzalandiranso chilango chonga chomwe Chauta adzalange nacho mtundu wina uliwonse wa anthu osapita kukachita chikondwerero chamisasa. Chimenechi ndicho chidzakhale chilango cha Aejipito ndiponso cha mtundu uliwonse wa anthu amene sadzachita nao chikondwerero chamisasacho. Pa tsiku limenelo pa mabelu ovala akavalo ankhondo padzalembedwa mau akuti, “Woperekedwa kwa Chauta.” Ndipo mbiya za ku Nyumba ya Chauta nazonso zidzakhala zoyera ngati mbale zakuguwa. Mbiya iliyonse ya ku Yerusalemu ndi ku Yuda idzakhala yoperekedwa kwa Chauta Wamphamvuzonse. Onse opereka nsembe ku Yerusalemu adzagwiritsa ntchito mbiyazo pophika nyama za nsembe. Nthaŵi imeneyo ikadzafika, sipadzaonekanso wamalonda aliyense m'Nyumba ya Chauta Wamphamvuzonse. Nawu uthenga wa Chauta kwa Aisraele kudzera mwa Malaki. Chauta akuti, “Ndakukondani inu.” Koma inu mumati. “Kodi mwatikonda motani?” Chauta akunena kuti, “Kodi suja Esau ndi mbale wake wa Yakobe? Komabe ndakonda Yakobe, koma Esau ndadana naye. Dziko lake lamapiri ndalisandutsa chipululu, dziko limene ndidampatsa ndalisandutsa la nkhandwe zam'chipululu.” Mwina Aedomu adzanena kuti, “Mulungu adapasula nyumba zathu, komabe ife tidzazimanganso.” Koma Chauta Wamphamvuzonse adzati, “Alekeni amangenso, Ine ndidzazigwetsanso. Anthu adzalitchula dziko loipa, la anthu amene Chauta adaŵatemberera mpaka muyaya.” Inu, Aisraele, mudzaziwona zimenezi ndi maso anu. Inu nomwe mudzati, “Ukulu wa Chauta umafika ngakhale kunja kwa malire a Aisraele.” Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Mwana amapatsa ulemu bambo wake ndipo kapolo amaopa mbuye wake. Ngati Ine ndine bambo wanu, nanga ulemu wanga uli kuti? Ngati ndine mbuye wanu, nanga kundiwopa kuli kuti, Ansembe inu, amene mumanyoza dzina langa. Komabe mumanena kuti, kodi dzina lanu timalinyoza bwanji? Mumalinyoza pakupereka chakudya chosayenera pa guwa langa lansembe. Inu mumafunsabe kuti, kodi ife takunyozani bwanji? Mwandinyoza pakuganiza kuti tebulo la Chauta nlonyozeka.” Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Mukaperekera nsembe nyama zakhungu, kodi si cholakwa? Mukaperekera nsembe nyama zopunduka kapena zodwala, kodi si cholakwa? Bwanamkubwa wanu mutampatsa mphatso zotero, kodi angazilandire? Kodi inuyo angakukomereni mtima?” Tsopano tayesani kupempha Mulungu kuti akuchitireni chifundo. Ndi mphatso zotere m'manja mwanu, kodi angakomere mtima aliyense mwa inu? Tsono Chauta Wamphamvuzonse akupitiriza kunena kuti, “Kudakakhala bwino kwambiri kuti wina mwa inu atsekeretu zitseko za Nyumba yanga, kuti mungayatse moto pachabe pa guwa langa. Sindikukondwera nanu, sindidzazilandira zopereka zanu. Dzina langa nlalikulu pakati pa mitundu ya anthu kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe. Kulikonse anthu amapereka nsembe zofukiza ndi mphatso zangwiro m'dzina langa. Pajatu dzina langa nlalikulu pakati pa mitundu ya anthu. “Koma inuyo mumalinyoza ponena kuti tebulo la Chauta nlachabechabe, ndipo chakudya chopereka pamenepo nchonyozeka.” Chauta Wamphamvuzonse akunenanso kuti, “Inu mumati, ‘Ha, kutopetsa zimenezi!’ Kenakanso nkumandinyodola. Mumabwera ndi nyama zakuba kapena zopunduka kapena zodwala ngati nsembe zanu, kodi Ine ndidzazilandira? Atembereredwe munthu wonyenga amene amayesa kuchita zimene adalumbirira popereka nsembe yoipa kwa Chauta, pamene ali nayo nkhosa yamphongo yabwino m'khola.” Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Ine ndine Mfumu yaikulu, ndipo dzina langa nlochititsa mantha pakati pa anthu a mitundu yonse.” Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Tsono ansembe inu, lamulo ili nlokhalira inu. Mukapanda kundimvera, mukapanda kulemekeza dzina langa, ndidzakutembererani. Zabwino zimene mumazilandira nazonso ndidzazitemberera. Ndithu, ndazitemberera kale chifukwa simudamvere ndi mtima wonse. “Ndidzalanga zidzukulu zanu. Ndidzakupakani ndoŵe za nsembe zanu kumaso, ndipo ndidzakutayani ku nkhuti ya ndoŵe. Apo mudzadziŵa kuti ndakupatsani lamulo ili kuti chipangano changa ndi ansembe, zidzukulu za Levi, chisaphwanyike. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. Ndidapangana nawo chipangano chopatsa moyo ndi mtendere. Ndidaŵapatsa zimenezi kuti azindiwopa, ndipo adandiwopadi namalemekeza dzina langa. Malangizo amene ankapereka anali oona, pakamwa pao sipankatuluka zosalungama. Ankamvana nane, ndipo ankayenda mokhulupirika ndi Ine, motero ankabweza anthu ambiri m'njira zao zoipa. “Pajatu ndi ntchito ya ansembe kuphunzitsa nzeru zoona za Mulungu, anthu ayenera kupita kwa iwo kuti akaphunzire zimene Ine ndifuna, chifukwa ansembewo ndiwo amithenga a Chauta Wamphamvuzonse. Koma inu ansembe mudasiya njira yanga. Mudaphunthwitsa anthu ambiri ndi zophunzitsa zanu. Mudaipitsa chipangano changa ndi Alevi. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. Nchifukwa chake Inenso ndakusandutsani onyozeka ndi achabechabe pamaso pa anthu, popeza kuti simudatsate njira zanga, ndipo mwakhala mukukondera poweruza milandu.” Kodi tonsefe suja tili ndi bambo mmodzi? Kodi suja adatilenga ndi Mulungu mmodzi? Chifukwa chiyani tsono tikuphwanya chipangano cha Mulungu ndi makolo athu posamakhulupirirana? Anthu a ku Yuda akhala osakhulupirika, ku Israele ndi ku Yerusalemu akhala akuchita zinthu zonyansa. Anthu a ku Yuda aipitsa Nyumba ya Chauta imene Iye amaikonda. Akhala akukwatira akazi opembedza milungu yachikunja. Wina aliyense wochita zimenezi Chauta amchotse ku banja la Yakobe. Asakhale nawonso ndi anthu opereka nsembe kwa Chauta Wopambanazonse. Zina zimene mumachita ndi izi: mumadandaula ndi kulira kwambiri mpaka kukhathamiza guwa la Chauta ndi misozi, chifukwa Iye amakana kuyang'ana nsembe zanu, osafuna kulandira mphatso iliyonse yodzatula inu. Mumafunsa kuti, “Chifukwa chake nchiyani?” Chifukwa chake nchakuti Chauta anali mboni ya chipangano chimene udachita ndi mkazi wako woyamba. Sudakhulupirike kwa iye, ngakhale iyeyo ndiye mnzako ndi mkazi wako potsata chipanganocho. Kodi suja Mulungu adakulenga, iwe ndi mkazi wako, kukhala mmodzi, thupi ndi mzimu womwe? Nanga pakutero Mulunguyo ankafuna chiyani? Ankafunatu ana ompembedza Iye. Motero samala moyo wako ndipo khala wokhulupirika kwa mkazi wako woyamba. Chauta, Mulungu wa Israele, akunena kuti, “Ndimadana ndi kusudzulana. Ndimadana ndi munthu wochita zankhalwe zotere kwa mkazi wake. Choncho chenjerani, musakhale osakhulupirika. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.” Mwatopetsa Chauta ndi zolankhula zanu. Komabe mumati, “Kodi tamtopetsa bwanji?” Mwamtopetsa ponena kuti, “Aliyense wochita zoipa ndi wabwino pamaso pa Chauta, ndipo Iye amakondwera naye.” Kapenanso pofunsa kuti, “Ali kuti Mulungu wochita zolungamayo?” Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Ndidzatuma wamthenga wanga kuti akandikonzere njira. Kenaka mwadzidzidzi Chauta amene mukumfunafuna adzafika ku Nyumba yake. Wamthenga wa chipangano, amene mukumuyembekeza, suuyu akubwera. Kodi ndani adzatha kupirira pa tsiku la kubwera kwake? Kodi ndani adzatha kulimbikira iye akadzafika? “Pakuti adzakhala ngati moto wa mmisiri wapang'anjo, ndiponso ngati sopo wa munthu wochapa. Adzachita kukhalira pansi ngati mmisiri wapang'anjo woyeretsa siliva, ndipo adzayeretsa Alevi monga amayeretsera golide ndi siliva, mpaka kuti azidzapereka nsembe zoyenera kwa Chauta. Choncho nsembe za Yuda ndi za Yerusalemu zidzakondweretsa Chauta, monga zidaaliri masiku amakedzana.” Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Tsono ndidzakufikani pafupi kuti ndikuzengeni mlandu. Mosataya nthaŵi ndidzanena mau otsutsa mfiti, anthu achigololo, a umboni wonama, odyerera antchito ao, ovutitsa akazi ndi ana amasiye, ochita alendo zosalungama ndipo onse amene sandiwopa Ine. “Ine ndine Chauta, wosasinthika. Nchifukwa chake inu zidzukulu za Yakobe simudaonongeke. Kuyambira masiku a makolo anu mwakhala mukuphwanya malamulo anga, simudaŵatsate konse. Ngati mubwerera kwa Ine, Inenso ndidzabwerera kwa inu. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. Komabe inu mumati, ‘Kodi tingathe kubwerera bwanji?’ Ine ndikuti, Kodi munthu angathe kubera Mulungu? Komabe inu mumandibera. Inu mumati, ‘Kodi timakuberani bwanji?’ Ine ndikuti, Mumandibera pa zachikhumi zanu ndi zopereka zina. Ndinu otembereredwa nonsenu, mtundu wanu wonse, chifukwa choti mumandibera. Aliyense abwere ndi chachikhumi chathunthu ku Nyumba yanga, kuti m'menemo mukhale chakudya chambiri. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. Mundiyese tsono, ndipo muwone ngati sinditsekula zipata zakumwamba ndi kukugwetserani madalitso ochuluka. Ndidzaletsa tizilombo kuti tisadye mbeu zanu, mipesa yanu sidzaleka kubala. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. Motero anthu a mitundu yonse adzakutchulani odala, pakuti dziko lanu lidzakhala lokondweretsa. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.” Chauta akunena kuti, “Mwalankhula mau olasa onena Ine. Komabe mukuti, ‘Kodi takunenani zotani?’ Mwanena kuti, ‘Kutumikira Mulungu nkwachabe. Kodi pali phindu lanji kumatsata malamulo a Chauta Wamphamvuzonse, kapena kumaonetsa chisoni pamaso pake? Koma ife timayesa kuti anthu odzikuza ndiwo odala. Anthu ochita zoipa ndiwo amene amakhala pabwino, ngakhale akaputa Mulungu amapulumuka ndithu.’ ” Tsono oopa Chauta adayamba kukambirana, Chauta namamvetsera. Buku lachikumbutso lidalembedwa pamaso pake, lonena za amene ankaopa Chauta ndi kulemekeza dzina lake. Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Anthu amenewo adzakhala anga, adzakhala angaanga okondedwa pa tsiku limene ndidzalikonza. Ndidzaŵachitira chifundo monga m'mene munthu amachitira ndi mwana wake womtumikira. Pamenepo mudzaonanso kusiyana pakati pa anthu abwino ndi anthu oipa, pakati pa anthu otumikira Mulungu ndi osamtumikira.” Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Tsiku likubwera pamene anthu onse odzikuza ndi ochita zoipa adzapsa ngati chiputu m'ng'anjo. Tsiku limenelo adzapserereratu osatsalako muzu kapena nthambi. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. Koma inu amene mumaopa dzina langa, dzuŵa lachilungamo lidzakutulukirani lili ndi kuŵala kokuchiritsani. Mudzalumphalumpha mokondwa ngati ana a ng'ombe ochokera m'khola. Tsiku limene ndilikukonzalo mudzapondereza anthu oipa ngati phulusa ku mapazi anu. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. “Kumbukirani zophunzitsa za Mose mtumiki wanga, malamulo ndi malangizo amene ndidamulamula ku phiri la Horebu kuti auze Aisraele onse. “Koma lisanafike tsiku lalikulu loopsalo la Chauta, ndidzakutumizirani mneneri Eliya. Iyeyo adzayanjanitsa atate ndi ana ao, ana ndi atate ao, kuwopa kuti ndingadzabwere kudzatemberera dziko lanu kuti liwonongeke.” Yesu Khristu, makolo ake anali Davide ndi Abrahamu. Motsatanatsatana maina a makolo ake onse ndi aŵa: Abrahamu adabereka Isaki, Isaki adabereka Yakobe, Yakobe adabereka Yuda ndi abale ake. Yuda adabereka Perezi ndi Zera, mwa Tamara; Perezi adabereka Hezironi, Hezironi adabereka Ramu. Ramu adabereka Aminadabu, Aminadabu adabereka Nasoni, Nasoni adabereka Salimoni. Salimoni adabereka Bowazi mwa Rahabu, Bowazi adabereka Obede mwa Rute, Obede adabereka Yese, Yese adabereka mfumu Davide. Davide adabereka Solomoni, mwa amene poyamba adaali mkazi wa Uriya. Solomoni adabereka Rehobowamu, Rehobowamu adabereka Abiya, Abiya adabereka Asa. Asa adabereka Yehosafati, Yehosafati adabereka Yoramu, Yoramu adabereka Uziya. Uziya adabereka Yotamu, Yotamu adabereka Ahazi, Ahazi adabereka Hezekiya. Hezekiya adabereka Manase, Manase adabereka Amoni, Amoni adabereka Yosiya. Yosiya adabereka Yekoniya ndi abale ake, pa nthaŵi imene Aisraele adaatengedwa ukapolo kupita ku Babiloni. Aisraele atatengedwa ukapolo kupita ku Babiloni, Yekoniya adabereka Salatiele, Salatiele adabereka Zerubabele. Zerubabele adabereka Abihudi, Abihudi adabereka Eliyakimu, Eliyakimu adabereka Azoro. Azoro adabereka Zadoki, Zadoki adabereka Akimu, Akimu adabereka Eliudi. Eliudi adabereka Eleazara, Eleazara adabereka Matani, Matani adabereka Yakobe. Yakobe adabereka Yosefe, mwamuna wa Maria. Mariayu adabala Yesu, wotchedwa Khristu. Choncho panali mibadwo khumi ndi inai kuyambira pa Abrahamu mpaka pa mfumu Davide, mibadwo khumi ndi inai kuyambira pa Davideyo mpaka pa nthaŵi imene Aisraele adaatengedwa ukapolo kupita ku Babiloni, ndiponso mibadwo khumi ndi inai kuyambira pa nthaŵi yotengedwa ukapolo kupita ku Babiloni mpaka pa nthaŵi ya Khristu, Mpulumutsi wolonjezedwa uja. Kubadwa kwa Yesu Khristu kudaatere: amai ake Maria adaafunsidwa mbeta ndi Yosefe; koma asanaloŵane, Maria adaapezeka kuti ali ndi pathupi mwa mphamvu za Mzimu Woyera. Mwamuna wake Yosefe anali munthu wokonda chilungamo, komabe sadafune kumchititsa manyazi poyera. Nchifukwa chake adaganiza za kungothetsa mbeta ija osachitapo mlandu. Akulingalira zimenezi, mngelo wa Ambuye adamuwonekera m'maloto, namuuza kuti, “Yosefe, mwana wa Davide, usaope kumtenga Maria, mkazi wakoyu. Pathupi ali napopa padachitika ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu, chifukwa adzapulumutsa anthu ake ku machimo ao.” Zonsezi zidaatero kuti zipherezere zimene Ambuye adaalankhulitsa mneneri kuti, “Namwali wina wosadziŵa mwamuna adzatenga pathupi nkubala mwana wamwamuna. Mwanayo adzatchedwa dzina loti Imanuele,” ndiye kuti “Mulungu ali nafe.” Tsono Yosefe atadzuka, adachita monga momwe mngelo wa Ambuye uja adaamuuzira. Adamtenga Maria, mkazi wake uja, koma sadamdziŵe mpaka adabala mwana wamwamuna. Pambuyo pake Yosefe adatcha mwanayo dzina loti Yesu. Yesu adabadwira m'mudzi wa Betelehemu, m'dziko la Yudeya, pa nthaŵi imene Herode anali mfumu ya dzikolo. Ndiye kudaabwera akatswiri ena a nyenyezi ku Yerusalemu kuchokera kuvuma. Iwowo ankafunsa kuti, “Ali kuti mwana amene adabadwa kuti adzakhale Mfumu ya Ayuda? Ife tidaona nyenyezi yake ikutuluka kuvumaku, motero tabwera kudzampembedza.” Mfumu Herode atamva zimenezi, adavutika kwambiri ndipo anthu ena onse a m'Yerusalemu nawonso adavutika nazo. Tsono Herodeyo adasonkhanitsa akulu onse a ansembe ndi aphunzitsi onse a Malamulo a Mose, naŵafunsa kuti, “Kodi paja adati Mpulumutsi wolonjezedwa ndi Mulungu uja adzabadwira kuti?” Iwo adati, “M'mudzi wa Betelehemu ku Yudeya. Pajatu mneneri adalemba kuti, “ ‘Iwe Betelehemu wa m'dziko la Yuda, sindiwe wamng'ono konse pakati pa akulu olamulira Yuda. Pakuti kwa iwe kudzachokera mtsogoleri pamene adzalamulira anthu anga Aisraele.’ ” Pamenepo Herode adaŵaitanira paseri akatswiri a nyenyezi aja, naŵafunsitsa za nthaŵi yeniyeni imene adaaiwonera nyenyeziyo. Kenaka adaŵatumiza ku Betelehemu nkuŵauza kuti, “Pitani, kafunsitseni za mwanayo. Mukakampeza, mudzandidziŵitse, kuti inenso ndidzapite kukampembedza.” Anthu aja atamva mau a mfumu, adanyamuka. Nyenyezi imene adaaiwona kuvuma ija idaŵatsogolera mpaka idakafika nkukaima pamwamba pa malo amene panali mwanayo. Ataiwona nyenyeziyo, adasangalala kwabasi. Adaloŵa m'nyumba, naona mwanayo ali ndi Maria mai wake, ndipo adagwada nampembedza. Kenaka adamasula chuma chao, nampatsa mitulo ya golide, lubani ndi mafuta onunkhira a mure. Mulungu adaŵachenjeza m'maloto kuti asadzerekonso kwa Herode kuja. Motero adadzera njira ina pobwerera kwao. Atapita akatswiri a nyenyezi aja, mngelo wa Ambuye adaonekera Yosefe m'maloto. Adamuuza kuti, “Nyamuka, tenga mwanayu ndi mai wake, uthaŵire ku Ejipito. Ukakhale kumeneko mpaka ndidzakuuze, popeza kuti Herode azidzafunafuna mwanayu kuti amuphe.” Apo Yosefe adadzuka usiku womwewo, nkutenga mwanayo ndi mai wake kupita ku Ejipito. Adakhala kumeneko mpaka Herode atamwalira, kuti zipherezere zimene Ambuye adaalankhulitsa mneneri kuti, “Ndidaitana Mwana wanga kuti atuluke ku Ejipito.” Herode atazindikira kuti akatswiri a nyenyezi aja adampusitsa, adatuma anthu ku Betelehemu ndi ku midzi yonse yozungulira, kuti akaphe ana aamuna onse a zaka ziŵiri kapena kucheperapo. Zaka zimenezi adaaŵerengera potsata m'mene adaamvera kwa akatswiri aja za nthaŵi imene iwowo adaaiwonera nyenyeziyo. Pamenepo zidachitikadi zimene mneneri Yeremiya adaanena kuti, “Mau akumveka ku Rama, kulira ndi kubuma kwambiri: Rakele akulira ana ake. Akukana kumtonthoza, chifukwa ana ake asoŵa.” Herode atamwalira, mngelo wa Ambuye adaonekera Yosefe m'maloto ku Ejipito. Adamuuza kuti, “Nyamuka, tenga mwanayu ndi mai wake, ubwerere ku Israele. Aja ankafuna kumupha mwanayu adafa.” Apo Yosefe adanyamuka, nkutenga mwana uja ndi mai wake, kubwerera ku Israele. Koma atamva kuti Arkelao ndiye mfumu ya ku Yudeya m'malo mwa bambo wake Herode, adaopa kupita kumeneko. Tsono atalandira chenjezo kwa Mulungu m'maloto, adapita ku dera la Galileya. Kumeneko adakakhala ku mudzi wina dzina lake Nazarete, kuti zipherezere zimene aneneri adaanena kuti, “Adzatchedwa Mnazarete.” Pa masiku amenewo kudaabwera Yohane Mbatizi nayamba kulalika m'chipululu cha ku Yudeya. Ankati, “Tembenukani mtima chifukwa Mulungu ali pafupi kukhazikitsa ufumu wake tsopano.” Paja Yesaya ankanena za iyeyu pamene adaati, “Liwu la munthu wofuula m'chipululu: akunena kuti, ‘Konzani mseu wodzadzeramo Ambuye, ongolani njira zoti adzapitemo.’ ” Yohaneyo ankavala zovala za ubweya wangamira, ndipo ankamangira lamba wachikopa m'chiwuno. Chakudya chake chinali dzombe ndi uchi wam'thengo. Anthu ochokera ku Yerusalemu ndi ku dera lonse la Yudeya, ndi ku madera onse a pafupi ndi mtsinje wa Yordani ankadza kwa iye. Ndiye ankati iwo akaulula machimo ao, iye nkumaŵabatiza mu Mtsinje wa Yordaniwo. Ankaona Ayuda ambiri a m'gulu la Afarisi ndi la Asaduki akubwera kuti iye aŵabatize. Tsono iyeyo ankati, “Ana a njoka inu, adakuchenjezani ndani kuti muthaŵe chilango cha Mulungu chikudzachi? Chitanitu ntchito zosonyeza kuti mwatembenukadi mtima. Ndipo m'mitima mwanu musayerekeze zomanena kuti, ‘Atate athu ndi Abrahamu.’ Ndithu ndikunenetsa kuti Mulungu angathe kusandutsa ngakhale miyala ili apayi kuti ikhale ana a Abrahamu. Pali pano nkhwangwa ili kale patsinde pa mitengo. Choncho mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino, adzaudula nkuuponya pa moto. “Ine ndimakubatizani ndi madzi, kusonyeza kuti mwatembenuka mtima. Koma amene akubwera pambuyo panga ndi wamphamvu kuposa ine. Ameneyo ine ndine wosayenera ngakhale kunyamula nsapato zake. Iyeyo adzakubatizani mwa Mzimu Woyera ndiponso m'moto. Chopetera chake chili m'manja kuti apete tirigu wake. Tsono adzathira tirigu m'nkhokwe, koma mankhusu adzaŵatentha m'moto wosazimika.” Pa masiku amenewo Yesu adachoka ku Galileya kubwera kwa Yohane ku mtsinje wa Yordani, kuti Yohaneyo amubatize. Yohane poyesa kukana, adati, “Ndine amene ndiyenera kubatizidwa ndi Inuyo. Nanga mukubweranso kwa ine kodi?” Koma Yesu adamuyankha kuti, “Tsopano lino vomera, chifukwa ndi m'mene tiyenera kuchitira zonse zimene Mulungu akufuna.” Apo Yohane adavomera. Yesu atangobatizidwa, adatuluka m'madzimo. Pomwepo kuthambo kudatsekuka, ndipo adaona Mzimu wa Mulungu akutsika ngati nkhunda nkutera pa Iye. Tsono kuthamboko kudamveka mau akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga wapamtima. Ndimakondwera naye kwambiri.” Zitatha izi, Mzimu Woyera adatsogolera Yesu kupita ku chipululu kuti Satana akamuyese. Pa masiku makumi anai Yesu adasala zakudya usana ndi usiku, ndipo pambuyo pake adamva njala. Tsono Woyesa uja adadza namuuza kuti, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, lamulani miyala ili apayi kuti isanduke chakudya.” Koma Yesu adati, “Malembo akuti, “ ‘Munthu sangakhale moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mau onse olankhula Mulungu.’ ” Pambuyo pake Satana adatenga Yesu kupita naye ku Yerusalemu, Mzinda Wopatulika, nakamuimika pamwamba penipeni pa Nyumba ya Mulungu. Adamuuza kuti, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, mudziponye pansi. Paja Malembo akuti, “ ‘Mulungu adzalamula angelo ake kuti akusamaleni, iwo adzakunyamulani m'manja mwao, kuti mapazi anu angapweteke pa miyala.’ ” Koma Yesu adati, “Malembo akutinso, ‘Usaŵayese Ambuye, Mulungu wako.’ ” Potsiriza Satana adatenga Yesu kupita naye pa phiri lalitali kwambiri, ndipo adamuwonetsa maufumu onse a pansi pano ndi ulemerero wake. Tsono adamuuza kuti, “Zonsezi ndidzakupatsani mukagwada pansi ndi kundipembedza.” Apo Yesu adati, “Choka, Satana! Paja Malembo akuti, ‘Uzipembedza Ambuye, Mulungu wako, ndipo uziŵatumikira Iwo okha.’ ” Pamenepo Satana adamsiya, angelo nkubwera kumadzamutumikira Yesuyo. Yesu atamva kuti Yohane adamponya m'ndende, adabwerera ku Galileya. Adachokako ku Nazarete, nakakhala ku Kapernao, mzinda wina wa m'mbali mwa nyanja ku dera la Zebuloni ndi Nafutali. Zidaatero kuti zipherezere zimene mneneri Yesaya adaanena kuti, “Iwe dziko la Zebuloni ndi iwe dziko la Nafutali, ku njira yakunyanja, patsidya pa Yordani, iwe Galileya, dziko la anthu akunja! Anthu okhala mu mdima aona kuŵala kwakukulu. Anthu okhala m'dziko la mdima wabii wa imfa, kuŵala kwaŵaonekera.” Kuyambira nthaŵi imeneyo Yesu adayamba kulalika kuti, “Tembenukani mtima, chifukwa ufumu wakumwamba wayandikira.” Yesu akuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, adaona anthu aŵiri pachibale pao: Simoni wotchedwa Petro, ndi mbale wake Andrea, akuponya khoka m'nyanjamo, popeza kuti anali asodzi. Yesu adaŵauza kuti, “Inu, munditsate, ndikakusandutseni asodzi a anthu.” Pomwepo iwo adasiya makoka ao, namamtsatadi. Atapitirira pamenepo, Yesu adaona enanso aŵiri pachibale pao: Yakobe ndi Yohane, ana a Zebedeo. Iwo anali m'chombo pamodzi ndi bambo waoyo, akukonza makoka ao, Yesu nkuŵaitana. Pomwepo iwowo adasiya chombo chao ndi bambo wao uja, namatsata Yesu. Yesu adayendera dziko lonse la Galileya akuphunzitsa m'nyumba zamapemphero ndi kulalika Uthenga Wabwino wonena za ufumu wakumwamba. Ankachiritsanso nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao zam'thupi. Mbiri yake idabuka m'dziko lonse la Siriya, kotero kuti anthu ankabwera kwa Iye ndi odwala onse ovutika ndi nthenda ndi zoŵaŵa zosiyanasiyana, ogwidwa ndi mizimu yoipa, akhunyu ndi opunduka, Iye nkumaŵachiritsa. Anthu ambirimbiri ankamutsata kuchokera ku Galileya, ku dera lotchedwa Mizinda Khumi, ku Yerusalemu, ku Yudeya ndi kutsidya kwa mtsinje wa Yordani. Yesu poona chikhamu cha anthu chija, adakwera pa phiri. Iye atakakhala pansi, ophunzira ake adamtsatira pomwepo. Kenaka adayamba kuŵaphunzitsa, adati, “Ngodala anthu amene ali osauka mumtima mwao, pakuti Ufumu wakumwamba ndi wao. Ngodala anthu amene akumva chisoni, pakuti Mulungu adzaŵasangalatsa. Ngodala anthu ofatsa, pakuti Mulungu adzaŵapatsa dziko la pansi pano kuti likhale lao. Ngodala anthu amene akumva njala ndi ludzu lofuna chilungamo, pakuti Mulungu adzakwaniritsa zofuna zao. Ngodala anthu ochitira anzao chifundo, pakuti iwonso Mulungu adzaŵachitira chifundo. Ngodala anthu oyera mtima, pakuti adzaona Mulungu. Ngodala anthu odzetsa mtendere, pakuti Mulungu adzaŵatcha ana ake. Ngodala anthu ozunzidwa chifukwa cha kuchita chilungamo, pakuti Ufumu wakumwamba ndi wao. “Ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani ndi kukunyengezerani zoipa zamitundumitundu chifukwa cha Ine. Sangalalani, kondwerani, chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu Kumwamba. Paja ndi m'menenso anthu ankazunzira aneneri amene analipo kale inu musanabadwe. “Inu ndinu mchere wa dziko lapansi. Koma ngati mcherewo watha mphamvu, mphamvu zakezo nkuzibwezeranso nchiyani? Ulibenso ntchito mpang'ono pomwe, koma kungoutaya kunja basi, anthu nkumauponda. “Inu ndinu kuŵala kounikira anthu onse. Mudzi wokhala pamwamba pa phiri sungabisike. Munthu sati akayatsa nyale, nkuivundikira ndi mbiya. Koma amaiika pa malo oonekera, ndipo imaunikira anthu onse amene ali m'nyumbamo. Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba. “Musamaganiza kuti ndidadzathetsa Malamulo a Mose ndiponso zophunzitsa za aneneri. Inetu sindidadzere kudzaŵathetsa, koma kudzaŵafikitsa pachimake penipeni. Ndithu ndikunenetsa kuti thambo ndi dziko lapansi zisanathe, sipadzachoka kalemba nkakang'ono komwe kapena kankhodolera pa Malamulowo, mpaka zonse zitachitika. Choncho aliyense wonyozera limodzi mwa malamulo ameneŵa, ngakhale laling'ono chotani, nkumaphunzitsa anthu ena kuti azitero, adzakhala wamng'ono ndithu mu Ufumu wakumwamba. Koma aliyense amene amaŵatsata nkumaphunzitsa anthu ena kuti azitero, adzakhala wamkulu mu Ufumu wakumwamba. Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti ngati kukhulupirika kwanu sikuposa kukhulupirika kwa aphunzitsi a Malamulo ndi kwa Afarisi, simudzaloŵa konse mu Ufumu wakumwamba. “Mudamva kuti anthu akale aja adaaŵalamula kuti, ‘Usaphe. Aliyense wopha mnzake adzayenera kuzengedwa ku bwalo lamilandu,’ Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti aliyense wopsera mtima mbale wake adzayenera kuzengedwa ku bwalo lamilandu. Aliyense wonena mnzake kuti, ‘Wopandapake iwe,’ adzayenera kuzengedwera ku Bwalo Lapamwamba. Ndipo aliyense wonena mnzake kuti, ‘Chitsiru,’ adzayenera kukaponyedwa ku moto wa Gehena. “Nchifukwa chake ngati wabwera ndi chopereka chako ku guwa, nthaŵi yomweyo nkukumbukira kuti mnzako wina ali nawe nkanthu, siya chopereka chakocho kuguwa komweko, ndipo pita, kayambe wayanjana naye mnzakoyo. Pambuyo pake ndiye ubwere kudzapereka chopereka chako chija. “Uziyanjana msanga ndi mnzako wamlandu, mukali pa njira yopita ku bwalo lamilandu, kuwopa kuti angakakupereke kwa woweruza, woweruzayo angakakupereke kwa msilikali, ndipo msilikaliyo angakakuponye m'ndende. Ndithu ndikunenetsa kuti sudzatulukamo mpaka utalipira zonse. “Mudamva kuti anthu akale aja adaaŵalamula kuti, ‘Usachite chigololo.’ Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti munthu aliyense woyang'ana mkazi ndi kumkhumba, wachita naye kale chigololo mumtima mwake. Ngati diso lako la ku dzanja lamanja likuchimwitsa, likolowole nkulitaya. Ndi bwino koposa kuti utayepo chiwalo chako chimodzi, kusiyana nkuti thupi lako lonse aliponye ku Gehena. Ndipo ngati dzanja lako lamanja likuchimwitsa, lidule nkulitaya. Ndi bwino kuti utayepo chiwalo chako chimodzi, kupambana kuti thupi lako lonse likaponyedwe ku Gehena.” “Anthu akale aja adaaŵalamulanso kuti, ‘Ngati munthu asudzula mkazi wake, ampatse mkaziyo kalata yachisudzulo.’ Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti aliyense amene asudzula mkazi wake, osati chifukwa cha chigololo, akumchititsa chigololo mkaziyo ngati akwatiwanso. Ndipo amene akwatira mkazi wosudzulidwayo, nayenso akuchita chigololo. “Mudamvanso kuti anthu akale aja adaaŵalamula kuti, ‘Usalumbire monama, koma uchitedi zimene udaŵalonjeza Ambuye molumbira.’ Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti muleke nkulumbira komwe. Usalumbire kuti, ‘Kumwambadi!’ Paja Kumwamba kuli mpando waufumu wa Mulungu. Usalumbire kuti, ‘Pali dziko lapansi!’ Paja dziko lapansi ndi chopondapo mapazi ake. Usalumbire kuti, ‘Pali Yerusalemu!’ Paja Yerusalemu ndi mzinda wa Mfumu yaikulu. Usalumbire ngakhale pa mutu wako, pakuti sungathe kusandulitsa ndi tsitsi limodzi lomwe kuti likhale loyera kapena lakuda. Muzingoti, ‘Inde,’ kapena ‘Ai.’ Zimene muwonjezerepo nzochokera kwa Satana, Woipa uja. “Mudamva kuti anthu akale aja adaaŵalamula kuti, ‘Diso kulipa diso, dzino kulipa dzino.’ Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti munthu woipa osalimbana naye. Ngati munthu akumenya pa tsaya la ku dzanja lamanja, upereke linalonso. Munthu akakuzenga mlandu nafuna kukulanda mkanjo wako, umlole atengenso ndi mwinjiro wako womwe. Munthu akakukakamiza kuyenda naye mtunda umodzi, uyende naye mitunda iŵiri. Munthu akakupempha kanthu, uzimpatsa. Ndipo munthu akafuna kubwereka kanthu kwa iwe, usamkanize.” “Mudamva kuti anthu akale aja adaaŵalamula kuti, ‘Ukonde mnzako, ndi kudana ndi mdani wako.’ Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti muzikonda adani anu ndipo muziŵapempherera amene amakuzunzani. Mukatero mudzakhaladi ana a Atate anu amene ali Kumwamba. Paja Iwo amaŵalitsa dzuŵa lao pa anthu abwino ndi pa anthu oipa omwe, ndipo amagwetsera mvula anthu olungama ndi osalungama omwe. Ngati mukonda okhawo amene amakukondani, mungalandire mphotho yanji? Kodi suja ngakhale okhometsa msonkho amachita chimodzimodzi? Ndipo ngati mupatsa moni abale anu okha, mwachitapo chiyani pamenepo choposa ena? Kodi suja ngakhale akunja amachita chimodzimodzi? Nchifukwa chake monga Atate anu akumwamba ali abwino kotheratu, inunso mukhale abwino kotheratu. “Chenjerani, musachite ntchito zanu zabwino pamaso pa anthu ndi cholinga choti akuwoneni. Mukatero, simudzalandira mphotho kwa Atate anu amene ali Kumwamba. “Nchifukwa chake pamene mukupereka zachifundo, musachite modziwonetsera, monga amachitira anthu achiphamaso aja m'nyumba zamapemphero ndiponso m'miseu yam'mizinda. Iwoŵa amachita zimenezi kuti anthu aŵatame. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao. Koma iwe ukamapereka zachifundo, dzanja lako lamanzere lisadziŵe zimene dzanja lako lamanja likuchita. Ukatero, zachifundo zakozo zidzakhala zodziŵa iwe wekha. Tsono Atate ako amene amaona zobisika adzakupatsa mphotho. “Pamene mukupemphera, musachite monga anthu achiphamaso aja. Iwowo amakonda kuimirira ndi kupemphera m'nyumba zamapemphero ndi pa mphambano za miseu yam'mizinda. Amachita zimenezi kuti anthu aŵaone. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao. Koma iwe, pamene ukuti upemphere, loŵa m'chipinda chako, tseka chitseko, ndipo upemphere kwa Atate ako amene ali osaoneka. Tsono Atate ako amene amaona zobisika adzakupatsa mphotho. “Pamene mukupemphera, musamangobwerezabwereza mau monga amachitira anthu akunja. Iwowo amayesa kuti akachulukitsa mau choncho, ndiye pamene Mulungu aŵamvere. Inu musamatero ai, pakuti Atate anu amadziŵa zimene mukusoŵa, inu musanapemphe. Nchifukwa chake popemphera muziti, “Atate athu akumwamba, dzina lanu lilemekezedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwechonso pansi pano. Mutipatse ife lero chakudya chathu chamasikuwonse. Mutikhululukire ife machimo athu, monga ifenso takhululukira otilakwira. Ndipo musalole kuti tigwe m'zotiyesa, koma mutipulumutse kwa Woipa uja.” [Pakuti ufumu, mphamvu ndi ulemerero ndi zanu kwamuyaya. Amen.] “Ndithu ngati mukhululukira anthu machimo ao, Atate anu akumwamba adzakukhululukirani inunso. Koma ngati simukhululukira anthu machimo ao, Atate anunso sadzakukhululukirani machimo anu. “Pamene mukusala zakudya, musamaonetsa nkhope zachisoni monga amachitira anthu achiphamaso aja. Iwo amaipitsa nkhope kuti anthu aone kuti akusala zakudya. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao. Koma iwe, pamene ukusala zakudya, samba m'maso nkudzola mafuta kumutu, kuti anthu asadziŵe kuti ukusala zakudya. Koma Atate ako amene ali osaoneka ndiwo adziŵe. Ndipo Atate akowo amene amaona zobisika, adzakupatsa mphotho. “Musadziwunjikire chuma pansi pano, pamene njenjete ndi dzimbiri zimaononga, ndiponso mbala zimathyola ndi kuba. Koma mudziwunjikire chuma Kumwamba, kumene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndiponso mbala sizithyola ndi kuba. Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko. “Maso ndiwo nyale zounikira thupi la munthu. Ngati maso ako ali bwino, m'thupi mwako monse mumakhala kuŵala. Koma ngati maso ako sali bwino, m'thupi mwako monse mumakhala mdima. Tsono ngati kuŵala kumene kuli mwa iwe kusanduka mdima, mdima wakewo ndi wochita kuti goo! “Munthu sangathe kutumikira mabwana aŵiri, pakuti kapena adzadana ndi mmodzi nkukonda winayo, kapena adzadzipereka kwa mmodzi nkumanyoza winayo. Simungathe kutumikira onse aŵiri, Mulungu ndi chuma. “Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti musamadera nkhaŵa moyo wanu, kuti mudzadyanji, kapena mudzamwanji, kapena thupi lanu, kuti mudzavalanji. Kodi suja moyo umaposa chakudya? Kodi suja thupi limaposa zovala? Onani mbalame zamumlengalenga. Sizifesa kapena kukolola kapena kututira m'nkhokwe ai. Komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengowapatali kuposa mbalame? Ndani mwa inu ndi maganizo ankhaŵa angathe kuwonjezera ngakhale tsiku limodzi pa moyo wake? “Ndipo mumaderanji nkhaŵa ndi zovala? Onani maluŵa akuthengo m'mene amakulira. Sagwira ntchito kapena kuwomba nsalu ai. Komatu kunena zoona, ngakhale mfumu Solomoni yemwe, mu ulemerero wake wonse, sankavala zokongola kulingana ndi limodzi lomwe mwa maluŵa ameneŵa. Tsono ngati Mulungu amaveka motere udzu wakuthengo, umene ungokhalapo lero lokha, maŵa lino nkuponyedwa pa moto, nanji inuyo, angapande kukuvekani, inu a chikhulupiriro chochepanu? “Nchifukwa chake musamada nkhaŵa nkumanena kuti, ‘Tidzadyanji? Tidzamwanji? Tidzavalanji?’ Paja zimenezi amazifunafuna ndi anthu akunja. Atate anu akumwamba amadziŵa kuti mukuzisoŵa zonsezi. Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso. Motero musadere nkhaŵa zamaŵa. Zamaŵa nzamaŵa. Tsiku lililonse lili ndi zovuta zake zokwanira. “Musamaweruza anthu ena kuti ndi olakwa, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni. M'mene inu mumaweruzira ena, ndi m'menenso Mulungu adzakuweruzirani inuyo. Ndipo muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu. Umaoneranji kachitsotso kamene kali m'maso mwa mnzako, koma osaganizako za chimtengo chimene chili m'maso mwako momwe? Ungamuuze bwanji mbale wako kuti, ‘Taima ntakuchotsa kachitsotso kali m'maso mwakoka,’ pamene m'maso mwako momwe muli chimtengo? Iwe wachiphamaso, yamba wachotsa chimtengo m'maso mwako, pamenepo ndiye udzatha kupenya bwino nkukachotsa kachitsotso kamene kali m'maso mwa mbale wako. “Musamapatsa agalu zinthu zopatulika, kapena kuponyera nkhumba ngale zamtengowapatali, kuwopa kuti zingazipondereze, kenaka nkukutembenukirani ndi kukukadzulani. “Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani. Paja munthu amene amapempha, ndiye amalandira; amene amafunafuna, ndiye amapeza; ndipo amene amagogoda, ndiye amamtsekulira. Ndani mwa inu, mwana wake atampempha buledi, iye nkumupatsa mwala? Kapena atampempha nsomba, iye nkumupatsa njoka? Tsono ngati inu, nkuipa kwanuku, mumadziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanji Atate anu amene ali Kumwamba, angalephere bwanji kupereka zinthu zabwino kwa amene aŵapempha? Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa. “Loŵerani pa chipata chophaphatiza. Pajatu chipata choloŵera ku chiwonongeko nchachikulu, ndipo njira yake ndi yofumbula, nkuwona anthu amene amadzerapo ndi ambiri. Koma chipata choloŵera ku moyo nchophaphatiza, ndipo njira yake ndi yosautsa, nkuwona anthu amene amaipeza ndi oŵerengeka. “Chenjera nawoni aneneri onyenga. Amadza kwa inu ali ndi maonekedwe ofatsa ngati nkhosa, koma m'kati mwao ndi mimbulu yolusa. Mudzaŵadziŵira zochita zao. Kodi mitengo yaminga nkubala mphesa? Kodi mitula nkubala nkhuyu? Chonchonso mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo woipa umabala zipatso zoipa. Mtengo wabwino sungabale zipatso zoipa, kapena mtengo woipa kubala zipatso zabwino ai. Mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino, amaudula nkuuponya pa moto. Choncho mudzaŵadziŵira zochita zao. “Si munthu aliyense womangonditi ‘Ambuye, Ambuye’ amene adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba ai. Koma adzaloŵe ndi wochita zimene Atate anga akumwamba afuna. Pa tsiku lachiweruzo anthu ambiri azidzanena kuti, ‘Ambuye, Ambuye, kodi suja ife tinkalalika mau a Mulungu m'dzina lanu? Suja tinkatulutsa mizimu yonyansa potchula dzina lanu? Suja tinkachita ntchito zamphamvu zambiri m'dzina lanu?’ Apo Ine ndidzaŵauza poyera kuti, ‘Sindidaakudziŵani konse. Chokani apa, anthu ochita zoipa.’ “Munthu aliyense womva mau angaŵa nkumaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu wanzeru amene adaamanga nyumba yake pa thanthwe. Kudagwa mvula, mitsinje idadzaza, ndipo chimphepo chidadza nkuwomba pa nyumbayo. Koma siidagwe, chifukwa chakuti adaaimanga polimba. Koma aliyense wongomva mau angaŵa, osaŵagwiritsa ntchito, ali ngati munthu wopusa amene adaamanga nyumba yake pa mchenga. Kudagwa mvula, mitsinje idadzaza, ndipo chimphepo chidadza nkuwomba pa nyumbayo, ndipo idagwa. Kugwa kwake kunali koopsa.” Yesu atatsiriza kunena zimenezi, anthu onse aja adadabwa ndi kaphunzitsidwe kake, chifukwa ankaŵaphunzitsa monga munthu waulamuliro osati monga m'mene ankachitira aphunzitsi a Malamulo. Yesu atatsika kuphiri kuja, anthu ambirimbiri adamtsatira. Tsono munthu wina wakhate adadzamugwadira nati, “Ambuye, mutafuna mungathe kundichiritsa.” Yesu adatambalitsa dzanja nkumukhudza, nati, “Chabwino, ndikufuna, chira!” Pomwepo khate lake lija lidatha, ndipo adachiradi. Tsono Yesu adamuuza kuti, “Chenjera, usakambire wina aliyense zimenezi. Ingopita, ukadziwonetse kwa wansembe, ndipo ukapereke nsembe adalamula Mose ija. Imeneyi ikhale yotsimikizira anthu onse kuti wachiradi.” Pamene Yesu ankaloŵa m'mudzi wa Kapernao, mkulu wina wolamulira gulu la asilikali 100 achiroma adadza kwa Iye. Adampempha kuti, “Ambuye, wantchito wanga ali gone kunyumbaku. Sakutha kuyenda, ndipo akumva kupweteka kwambiri.” Yesu adamuuza kuti, “Chabwino, ndibwera kudzamchiritsa.” Koma mkulu uja adati, “Ambuye, sindili woyenera kuti Inu nkuloŵa m'nyumba mwanga. Mungonena mau okha, ndipo wantchito wangayo achira. Inetu ndili ndi akuluakulu ondilamulira, komanso ndili ndi asilikali amene ineyo ndimaŵalamulira. Ndimati ndikauza wina kuti, ‘Pita,’ amapitadi. Ndikauzanso wina kuti, ‘Bwera,’ amabweradi. Ndipo ndikauza kapolo wanga kuti, ‘Chita chakuti,’ amachitadi.” Yesu atamva zimenezi, adachita chidwi, ndipo adauza anthu amene ankamutsata aja kuti, “Kunena zoona, ngakhale pakati pa Aisraele sindidapeze chikhulupiriro chotere. Ndithu ndikunenetsa kuti ambiri adzabwera kuchokera kuvuma ndi kuzambwe nadzakhala nao pa phwando mu Ufumu wakumwamba pamodzi ndi Abrahamu, Isaki ndi Yakobe. Koma chonsecho amene akadayenera kukhala mu Ufumuwo, adzaŵaponya kunja, ku mdima. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano chifukwa cha zoŵaŵa.” Kenaka pouza mkulu wa asilikali uja Yesu adati, “Inu pitani bwino, zikuchitikireni monga momwe mwakhulupiriramu.” Tsono wantchito wake uja adachira nthaŵi yomweyo. Pamene Yesu adakaloŵa m'nyumba ya Petro, adaona apongozi a Petro ali gone, akudwala malungo. Adakhudza amaiwo pa dzanja, ndipo malungowo adatha. Pomwepo amai aja adadzuka nayamba kukonzera Yesu chakudya. Madzulo amenewo, anthu adabwera kwa Yesu ndi anzao ambiri ogwidwa ndi mizimu yoipa. Yesu adaitulutsa mizimuyo ndi mau chabe, ndipo onse amene ankadwala adaŵachiritsa. Adachita zimenezi kuti zipherezere zimene mneneri Yesaya adaanena zakuti, “Iye adatenga zofooka zathu, adasenza nthenda zathu.” Pamene Yesu adaona chinamtindi cha anthu amene adaamuzinga, adauza ophunzira ake kuti, “Tiyeni tiwolokere tsidya linalo.” Koma nthaŵi yomweyo padafika mphunzitsi wina wa Malamulo namuuza kuti, “Aphunzitsi, ndizikutsatani kulikonse kumene muzipita.” Yesu adamuyankha kuti, “Nkhandwe zili ndi michembo yake, mbalame zili ndi zisa zake, koma Mwana wa Munthu alibe mpogoneka mutu pomwe.” Wophunzira wake wina adauza Yesu kuti, “Ambuye, mundilole ndiyambe ndakaika maliro a atate anga.” Koma Yesu adamuuza kuti, “Iweyo unditsate, aleke akufa aziika akufa anzao.” Yesu adaloŵa m'chombo, ndipo ophunzira ake adatsagana naye. Tsono padauka namondwe woopsa panyanjapo, kotero kuti mafunde ankaloŵa m'chombomo. Koma Yesu anali m'tulo. Pamenepo ophunzira ake aja adamudzutsa, adati, “Ambuye, tipulumutseni, tikumiratu!” Apo Yesu adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukuchita mantha, inu anthu a chikhulupiriro chochepa?” Atatero adaimirira nkudzudzula mphepoyo ndi nyanjayo, kenaka padagwa bata lalikulu ndithu. Ophunzira aja adazizwa nati, “Kodi ameneyu ndi munthu wotani kuti ngakhale mphepo ndi nyanja yomwe zizimumvera?” Yesu atafika ku tsidya la nyanja, ku dera la Agadara, anthu aŵiri ogwidwa ndi mizimu yoipa adadzakumana naye kuchokera ku manda. Anali aukali kwambiri, kotero kuti panalibe munthu ndi mmodzi yemwe wotha kudzera njira imeneyo. Mwadzidzidzi anthuwo adayamba kufuula kuti, “Kodi takuputani chiyani, Inu Mwana wa Mulungu? Kodi mwabwera kuno kudzatizunza nthaŵi isanakwane?” Pafupi pomwepo pankadya gulu lalikulu la nkhumba. Tsono mizimu yoipa ija idapempha Yesu kuti, “Mukatitulutsa, bwanji mutitume kuti tikaloŵe m'gulu la nkhumba zili apozo.” Yesu adaiwuza kuti, “Chabwino, pitani!” Iyo idatuluka nkukaloŵadi m'nkhumbazo. Pomwepo gulu lonselo lidaguduka kutsika chitunda chija mwaliŵiro, nkukadziponya m'nyanja mpaka kufera m'madzimo. Oŵeta nkhumbazo adathaŵa. Atakaloŵa mu mzinda, adakasimbira anthu zonse zimene zidachitika, ndiponso zimene zidaŵaonekera ogwidwa ndi mizimu yoipa aja. Pamenepo anthu onse amumzindamo adatuluka kuti akakumane ndi Yesu. Tsono atampeza, adamupempha kuti achoke ku dera laolo. Yesu adaloŵa m'chombo naoloka nyanja, nkukafika ku mzinda wakwao. Kumeneko anthu ena adabwera kwa Iye ndi munthu wa ziwalo zakufa ali chigonere pa machira. Poona chikhulupiriro chao, Yesu adauza munthu wa ziwalo zakufayo kuti, “Limba mtima, mwana wanga, machimo ako akhululukidwa.” Apo aphunzitsi ena a Malamulo adayamba kudzifunsa mumtima mwao kuti, “Munthu ameneyu akuchita chipongwe Mulungu.” Koma Yesu adaadziŵa zimene iwo ankaganiza, motero adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukuganiza zoipa mumtima mwanu? Chapafupi koposa nchiti, kunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kunena kuti, ‘Dzuka, yamba kuyenda?’ Koma kuti mudziŵe kuti Mwana wa Munthu ali nazo mphamvu pansi pano zokhululukira machimo, onani.” Pamenepo adauza wofa ziwalo uja kuti, “Iwe, dzuka, tenga machira ako, uzipita kumudzi.” Munthu uja adadzukadi namapita kwao. Anthu onse aja ataona zimenezi, adachita mantha, ndipo adatamanda Mulungu amene adapatsa anthu mphamvu zotere. Yesu atachoka pamenepo, adaona munthu wina, dzina lake Mateyo, ali pa ntchito m'nyumba ya msonkho. Adamuuza kuti, “Iwe, unditsate.” Iye adanyamuka nkumamutsatadi. Tsono pamene Yesu ankadya m'nyumba, kudabwera anthu ambiri okhometsa msonkho, ndi anthu ochimwa, kudzadya nao ndi Yesuyo ndi ophunzira ake. Pamene Afarisi adaona zimenezi, adafunsa ophunzira a Yesu kuti, “Bwanji aphunzitsi anu akudya pamodzi ndi okhometsa msonkho ndiponso ndi anthu ochimwa?” Yesu atamva zimenezo, adaŵayankha kuti, “Anthu amene ali bwino sasoŵa sing'anga ai, koma amene akudwala. Kamvetsetseni tanthauzo la mau a Mulungu aja akuti, ‘Ndimafuna chifundo, osati nsembe ai.’ Inetu sindidabwere kudzaitana anthu olungama, koma anthu ochimwa.” Pambuyo pake ophunzira a Yohane Mbatizi adabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Kodi bwanji ife ndi Afarisi timasala zakudya kaŵirikaŵiri, pamene ophunzira anu sasala nkomwe?” Yesu adati, “Kani anzake a mkwati angathe kumasala zakudya pamene mkwati ali nao pomwepo? Chosatheka! Koma idzafika nthaŵi pamene adzaŵachotsera mkwatiyo. Pamenepo ndiye azidzasala zakudya. Munthu satenga chigamba cha nsalu yatsopano, nkuchisokerera pa chovala chakale. Chigamba chotere chimakoka nkunyotsolako chovalacho, ndiye kung'ambika kwake kumakhala kwakukulu koposa kale. Ndiponso munthu sathira vinyo watsopano m'matumba achikopa akale. Chifukwa akatero, matumbawo amaphulika, vinyoyo natayika, matumbawo nkutha ntchito. Koma vinyo watsopano amamuthira m'matumba atsopanonso. Apo zonse ziŵiri zimasungika bwino.” Pamene Yesu ankakamba zimenezi, munthu wina wamkulu adadzamgwadira nati, “Mwana wanga wamkazi wamwalira tsopano apa. Chonde bwerani mudzamsanjike manja, kuti akhale ndi moyo.” Pamenepo Yesu adanyamuka, namtsatira pamodzi ndi ophunzira ake. Tsono panali mai wina amene adakhala akuvutika ndi matenda a msambo pa zaka khumi ndi ziŵiri. Iyeyu adafika cha kumbuyo kwa Yesu, nakhudza mphonje ya chovala chake. Mumtima mwake ankaganiza kuti, “Ndikangokhudza ngakhale chovala chake chokhacho, ndichira.” Pamenepo Yesu adacheuka, naona maiyo, ndipo adati, “Limbani mtima mai, chikhulupiriro chanu chakuchiritsani.” Nthaŵi yomweyo mai uja adachiradi. Pamene Yesu adafika kunyumba kwa mkulu uja, adaona anthu oimba zitoliro, ndiponso anthu ambiri obuma. Tsono Iye adaŵauza kuti, “Tatulukani! Mtsikanayutu sadamwalire ai, ali m'tulo chabe.” Pamenepo anthuwo adayamba kumseka monyodola. Koma onsewo atatulutsidwa, Yesu adaloŵa, nagwira mtsikanayo pa dzanja, iye nkuuka. Mbiri imeneyi idawanda m'dera lonselo. Pamene Yesu ankachoka kumeneko, anthu aŵiri akhungu adamtsatira. Ankafuula kuti, “Inu Mwana wa Davide, mutichitire chifundo.” Yesu ataloŵa m'nyumba, akhungu aja adadzampeza, Iye nkuŵafunsa kuti, “Kodi mukukhulupirira kuti ndingathe kuchita zimenezi?” Iwo adati, “Inde, Ambuye.” Apo Yesu adakhudza maso ao nati, “Zikuchitikireni monga momwe mwakhulupiriramo.” Pamenepo maso ao adaphenyuka. Tsono Yesu adaŵalamula mwamphamvu kuti, “Wina aliyense asazidziŵetu zimenezi.” Koma iwo adachoka pamenepo nkumakawanditsa mbiri yake ku dera lonselo. Pamene iwowo ankatuluka m'nyumbamo, anthu ena adabwera kwa Yesu ndi munthu wosatha kulankhula, chifukwa chogwidwa ndi mzimu woipa. Yesu atatulutsa mzimu woipawo, munthu uja adayamba kulankhula. Apo anthu onse adazizwa nati, “Nkale lonse Aisraele sadaziwone zotere.” Koma Afarisi adati, “Ameneyu amatulutsa mizimu yoipa ndi mphamvu zomupatsa mfumu ya mizimu yoipa ija.” Yesu adayendera mizinda ndi midzi yonse. Adanka naphunzitsa m'nyumba zao zamapemphero, nkumalalika Uthenga Wabwino wonena za Ufumu wakumwamba. Ndiponso ankachiritsa nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao zam'thupi. Pamene adaona makamu a anthu, adaŵamvera chifundo, chifukwa iwo anali olema ndi ovutika ngati nkhosa zopanda mbusa. Tsono adauza ophunzira ake kuti, “Dzinthu ndzochulukadi, achepa ndi antchito. Nchifukwa chake mupemphe Mwini dzinthu kuti atume antchito okatuta dzinthu dzakedzo.” Yesu adasonkhanitsa ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja, naŵapatsa mphamvu pa mizimu yoipitsa anthu, kuti aziitulutsa mwa anthuwo, ndiponso mphamvu zochiritsira nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao zam'thupi. Atumwi khumi ndi aŵiriwo maina ao ndi aŵa: Woyamba ndi Simoni, wotchedwa Petro, ndipo mbale wake Andrea; Yakobe, mwana wa Zebedeo, ndi mbale wake Yohane; Filipo ndi Bartolomeo; Tomasi ndi Mateyo, wokhometsa msonkho uja; Yakobe, mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo; Simoni, wa m'chipani chandale cha Azelote; ndiponso Yudasi Iskariote, amene pambuyo pake adapereka Yesu kwa adani ake. Anthu khumi ndi aŵiri ameneŵa Yesu adaŵatuma ndi malamulo akuti, “Musapite kwa anthu a mitundu ina kapena kukaloŵa m'mudzi uliwonse wa Asamariya ai. Koma makamaka mupite kwa Aisraele amene ali ngati nkhosa zotayika. Pitani, muzikalalika kuti, ‘Mulungu ali pafupi kukhazikitsa ufumu wake tsopano.’ Muzikachiritsa odwala, muzikaukitsa akufa, muzikachotsa khate, muzikatulutsa mizimu yoipa. Mwalandira mwaulere, kaperekeni mwaulere. Musatenge ndalama m'zikwama, kaya nzagolide, kaya nzasiliva, kaya nzakopala. Musatenge thumba lapaulendo, kapena mikanjo iŵiri, kapena nsapato, kapena ndodo. Paja wantchito ngwoyenera kulandira zosoŵa zake. “Pamene mwaloŵa mu mzinda kapena m'mudzi uliwonse, mufunsitse za munthu wofunadi kukulandirani. Mukakhale kunyumba kwake mpaka nthaŵi yochoka. Poloŵa m'nyumba, muzikanena kuti, ‘Mtendere ukhale ndi inu’. Tsono ngati anthu am'nyumbamo akulandiranidi, mtendere wanuwo ukhale nawo ndithu. Koma ngati anthu am'nyumbamo akana kukulandirani, mtendere wanuwo ubwerere kwa inu. Munthu aliyense akakana kukulandirani kapena kumvera mau anu, musanse fumbi la kumapazi kwanu potuluka m'nyumbamo kapena m'mudzimo. Ndithu ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo, Mulungu adzachitako chifundo polanga mudzi wa Sodomu ndi wa Gomora, koma osati polanga mudzi umenewo. “Mumvetse bwino! Ndikukutumani ngati nkhosa pakati pa mimbulu. Ndiye inu khalani ochenjera ngati njoka, ndi ofatsa ngati nkhunda. Anthu muchenjere nawo, pakuti adzakuperekani ku mabwalo amilandu, ndipo adzakukwapulani m'nyumba zao zamapemphero. Adzapita nanu kwa nduna ndi mafumu chifukwa cha Ine, mwakuti mudzandichitira umboni pamaso pao, ndi pa anthu a mitundu ina. Akadzakutengerani ku milandu, musadzade nkhaŵa nkumanena kuti, ‘Kodi tikakambe bwanji?’ Kapena kuti, ‘Kodi tikanene chiyani?’ Mudzapatsidwa pa nthaŵi imeneyo mau oti munene. Pajatu odzalankhula si ndinu ai, koma Mzimu wa Atate anu ndiye amene adzalankhula kudzera mwa inu. “Mbale azidzapereka mbale wake kuti aphedwe, bambo azidzapereka mwana wake. Ana adzaukira makolo ao, mpaka kuŵaphetsa. Anthu onse adzadana nanu chifukwa cha Ine. Koma yemwe adzalimbikire mpaka potsiriza, ameneyo ndiye adzapulumuke. Tsono akamadzakuzunzani ku mudzi wakutiwakuti, mukathaŵire ku mudzi wina. Ndithu ndikunenetsa kuti musanathe kuyendera midzi yonse ya Aisraele, Mwana wa Munthu adzakhala atabwera. Paja wophunzira saposa mphunzitsi wake, ndipo wantchito saposa mbuye wake ai. Kumkwanira wophunzira kuti alingane ndi mphunzitsi wake, ndiponso wantchito kuti alingane ndi mbuye wake. Tsono ngati mwini banja anthu adamutcha Belezebulu, nanji a m'banja mwake, kodi sadzaŵatcha maina oipa koposa apa? “Choncho inu musamaopa anthu. Kanthu kalikonse kovundikirika kadzaululuka, ndipo kalikonse kobisika kadzadziŵika. Zimene ndikukuuzirani m'chibisibisi, inu mukazilankhulire poyera, ndipo zimene mukuzimvera m'manong'onong'o, inu mukazilalikire pa madenga. Musamaŵaopa amene amapha thupi, koma mzimu sangathe kuupha. Makamaka muziwopa amene angathe kuwononga thupi ndi mzimu womwe m'Gehena. Suja amagulitsa atimba aŵiri kandalama kamodzi? Komabe palibe ndi m'modzi yemwe amene angagwe pansi, Atate anu osadziŵa. Inuyotu ngakhale tsitsi lomwe la kumutu kwanu adaliŵerenga lonse. Choncho musati muziwopa ai. Ndinu a mtengo woposa atimba ambiri. “Aliyense wondivomereza pamaso pa anthu, Inenso ndidzamuvomereza pamaso pa Atate anga amene ali Kumwamba. Koma aliyense wondikana pamaso pa anthu kuti Ine sandidziŵa, Inenso ndidzamkana pamaso pa Atate anga amene ali Kumwamba kuti sindimdziŵa. “Kodi mukuyesa kuti ndidadzapereka mtendere pansi pano? Sindidadzapereke mtendere ai, koma nkhondo. Inetu paja ndidadzalekanitsa mwana wamwamuna ndi bambo wake, mwana wamkazi ndi mai wake, mkazi ndi apongozi ake aakazi, mwakuti adani a munthu adzakhala a m'banja mwake omwe. “Munthu wokonda bambo wake kapena mai wake koposa Ine, ngwosayenera kukhala wophunzira wanga. Ndipo wokonda mwana wake wamwamuna kapena wamkazi koposa Ine, ngwosayenera kukhala wophunzira wanga. Amene sasenza mtanda wake ndi kumanditsata, ngwosayenera kukhala wophunzira wanga. Munthu woyesa kusunga moyo wake, adzautaya, ndipo wotaya moyo wake chifukwa cha Ine, adzausunga. “Munthu wokulandirani inu, amandilandira Ine ndemwe. Ndipo wondilandira Ine, amalandiranso Iye uja amene adandituma. Munthu wolandira nthumwi ya Mulungu chifukwa choti ndi nthumwi, adzalandira mphotho ya nthumwi ya Mulungu. Wolandira munthu wolungama chifukwa choti ngwolungama, adzalandira mphotho ya munthu wolungama. Ndipo aliyense wopatsa ngakhale chikho cha madzi ozizira kwa mmodzi mwa ophunzira angaŵa, chifukwa chakuti ndi wophunzira wanga, ndithu ndikunenetsa kuti ameneyo sadzalephera kulandira mphotho yake.” Yesu atatsiriza kulangiza ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja, adachoka kumeneko nkumakaphunzitsa ndi kulalika m'mizinda yao. Pamene Yohane Mbatizi anali m'ndende, adaamva zimene Khristu uja ankachita. Choncho adatuma ophunzira ake ena kwa Iye kukamufunsa kuti, “Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” Yesu adati, “Pitani, kamuuzeni Yohane zimene mukuzimva ndi kuziwona. Akhungu akupenya ndipo opunduka miyendo akuyenda; akhate akuchira ndipo agonthi akumva; akufa akuukitsidwa ndipo amphaŵi akumva Uthenga Wabwino. Ngwodala munthu amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.” Pamene amithenga a Yohane aja ankachoka, Yesu adayamba kufunsa makamu a anthu aja za Yohane kuti, “Kodi m'mene mudaapita ku chipululu, mudaati mukaona chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi? Nanga mudaati mukaona chiyani? Munthu wovala zofeŵa kodi? Iyai, anthu ovala zofeŵa amakhala m'nyumba za mafumu. Tanenanitu, mudaati mukaona chiyani? Mneneri kodi? Zoonadi, ndipo ndikunenetsa kuti mudakaona woposa mneneri amene. Ameneyu ndiye uja Malembo akunena zakeyu kuti, “ ‘Nayitu nthumwi yanga, ndikuituma m'tsogolo mwako, kuti ikakonzeretu njira yodzadzeramo iwe.’ Ndithu ndikunenetsa kuti mwa anthu onse amene adabadwa pansi pano, palibe ndi mmodzi yemwe woposa Yohane Mbatizi. Komabe ngakhale amene ali wamng'onong'ono mu Ufumu wakumwamba amampambana. Kuyambira pa nthaŵi ya Yohane Mbatizi mpaka tsopano anthu akhala akulimbana ndi Ufumu wa Kumwamba, ndipo ochita chamuna ndiwo amene akuulanda. Aneneri onse ndiponso Malamulo a Mose ankaneneratu za Ufumu umenewu mpaka nthaŵi ya Yohane Mbatizi. Ndipo ngati mukufunadi kukhulupirira zimenezi, Yohaneyo ndiye Eliya uja ankati adzabwerayu. Amene ali ndi makutu, amve! “Kaya anthu amakonoŵa ndingaŵafanizire ndi chiyani? Ali ngati ana okangana pa msika, ena akufunsa anzao kuti, “ ‘Tidaakuimbirani ng'oma yaukwati, bwanji inu osavina? Tidaabuma maliro, bwanji inu osalira?’ Paja Yohane Mbatizi atabwera, ankasala zakudya ndi zakumwa, anthu nkumati, ‘Adagwidwa ndi mzimu woipa.’ Mwana wa Munthu adabwera nkumadya ndi kumwa ndithu, anthu amvekere, ‘Tamuwonani, munthuyu ndi wadyera, chidakwa, ndiponso bwenzi la anthu amsonkho ndi anthu osasamala Malamulo.’ Komabe chilungamo cha nzeru za Mulungu chimatsimikizika ndi zochita zake.” Pambuyo pake Yesu adayamba kudzudzula midzi imene Iye adaaichitira zamphamvu zochuluka. Adaidzudzula chifukwa anthu ake anali osatembenuka mtima. Adati, “Uli ndi tsoka iwe Korazini! Uli ndi tsoka iwe Betsaida! Chifukwa zamphamvu zimene zidachitika mwa inu, achikhala zidaachitikira ku Tiro ndi ku Sidoni, bwenzi anthu ake atavala kale ziguduli nkudzithira phulusa, kuwonetsa kuti atembenukadi mtima. Koma ndikunenetsa kuti pa tsiku lachiweruzo, Mulungu adzachitako chifundo polanga Tiro ndi Sidoni, koposa polanga inu. Ndipo iwe Kapernao, kodi ukuyesa kuti adzakukweza mpaka Kumwamba? Iyai, adzakutsitsa mpaka ku Malo a anthu akufa. Chifukwa zamphamvu zimene zidachitika mwa iwe, achikhala zidaachitikira m'Sodomu, bwenzi mzindawo ukadalipo mpaka lero. Koma ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo Mulungu adzachitako chifundo polanga Sodomu koposa polanga iwe.” Pa nthaŵi imeneyo Yesu adati, “Atate, Mwini kumwamba ndi dziko lapansi, ndikukuyamikani kuti zinthuzi mudaululira anthu osaphunzira, nkubisira anthu anzeru ndi ophunzira. Chabwino Atate, pakuti mudafuna kutero mwa kukoma mtima kwanu. “Atate adaika zonse m'manja mwanga. Palibe wina wodziŵa Mwana kupatula Atate okha. Palibenso wina wodziŵa Atate kupatula Mwana yekha, ndiponso amene Mwanayo akufuna kumuululira. “Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu. Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.” Pa tsiku lina la Sabata Yesu ankadutsa m'minda ya tirigu. Ophunzira ake anali ndi njala, ndipo adayamba kuthyolako ngala za tirigu nkumadya. Pamene Afarisi adaona zimenezi, adauza Yesu kuti, “Taonani, ophunzira anu akuchita zimene siziloledwa pa tsiku la Sabata.” Iye adati, “Kani simudaŵerenge zimene adaachita Davide, pamene iye ndi anzake adaazingwa nayo njala? Suja adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, nkukadya buledi woperekedwa kwa Mulungu? Chonsecho buledi ameneyo kunali kosaloledwa kuti iyeyo kapena anzakewo nkumudya, koma ansembe okha. Kaya simudaŵerengenso m'Malamulowo kuti m'Nyumba ya Mulungu, pa tsiku la Sabata, ansembe amaphwanya lamulo lokhudza tsiku la Sabata, komabe saŵayesa olakwa? Ndipotu ndikunenetsa kuti pali wina pano woposa Nyumba ya Mulunguyo. Mukadadziŵa tanthauzo la mau a Mulungu aja akuti, ‘Ndimafuna chifundo, osati nsembe ai,’ sibwenzi mutaweruza kuti ndi olakwa anthu amene sadalakwe konse. Pajatu Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro wonse pa zokhudza tsiku la Sabata.” Yesu adachoka kumeneko nakaloŵa m'Nyumba yamapemphero. M'menemo munali munthu wopuwala dzanja. Tsono anthu ena amene ankafuna chifukwa choti akamnenezere Yesuyo, adamufunsa kuti, “Kodi Malamulo amalola kuchiritsa munthu pa tsiku la Sabata?” Yesu adaŵayankha kuti, “Ndani mwa inu atakhala ndi nkhosa imodzi, nkhosayo nkugwa m'dzenje pa tsiku la Sabata, angapande kuigwira nkuitulutsa? Nanji munthu, amene amaposa nkhosa kutalitali! Ndiye kutitu Malamulo amalola kuchita zabwino pa tsiku la Sabata.” Atatero, adalamula munthu uja kuti, “Tambalitsa dzanja lako.” Iye adalitambalitsa, ndipo dzanja lakelo lidakhalanso bwino ngati linzake. Pamenepo Afarisi aja adatuluka nakachita upo kuti apangane njira yophera Yesu. Yesu atamva za upowo, adachokako kumeneko. Anthu ambiri adamtsatira, ndipo Iye adaŵachiritsa onse amene ankadwala. Koma adaŵalamula kuti asakamuulule. Adaachita zimenezi kuti zipherezere zimene Mulungu adaalankhulitsa mneneri Yesaya kuti, “Nayu mtumiki wanga amene ndamsankha. Ndimamkonda, ndipo mtima wanga umasangalala naye kwambiri. Ndidzaika Mzimu wanga mwa iyeyo, ndipo adzalalika za chilungamo kwa anthu a mitundu ina. Iye sadzachita makani, kapena kufuula. Palibe munthu wodzamva mau ake m'miseu ya m'mizinda. Iye sadzatsiriza bango lothyoka, nyale yofuka sadzaizimitsa, mpaka atapambanitsa chilungamo. Ndipo anthu akunja adzamdalira.” Pambuyo pake anthu adadza kwa Yesu ndi munthu wakhungu, wosatha kulankhula, ndi woloŵedwa mizimu yoipa. Tsono Yesu adamchiritsa, kotero kuti adayamba kulankhula ndi kupenya. Anthu onse adazizwa kwambiri nkumanena kuti, “Kodi ameneyu sangakhale Mwana uja wa Davide?” Koma Afarisi atamva zimenezi adati, “Iyai, mphamvu zimene iyeyu amatulutsira mizimu yoipa sizichokeratu kwina, koma kwa Belezebulu, mkulu wa mizimu yoipayo.” Yesu adaadziŵa zimenezi, motero adaŵauza kuti, “Anthu a mu ufumu uliwonse akayamba kuukirana, ufumuwo kutha kwake nkomweko. Ndipo anthu a m'mudzi uliwonse kapena a m'banja lililonse akayamba kuukirana, mudzi wotere kapena banja lotere silingalimbe ai. Ngati a mu ufumu wa Satana atulutsana okhaokha, ndiye kuti agaŵikana. Nanga Satanayo ufumu wake ungalimbe bwanji? Inu mukuti Ineyo ndimatulutsa mizimu yoipa ndi mphamvu za Belezebulu, nanga ophunzira anu amaitulutsa ndi mphamvu za yani? Nchifukwa chake ophunzira anu omwewo ndi amene adzakuweruzeni kuti ndinu olakwa. Koma ngati Ine ndimatulutsa mizimu yoipa ndi mphamvu za Mzimu wa Mulungu, ndiye kuti Mulungu wayamba kukhazikitsa ufumu wake pakati panu. “Palibe munthu amene angathe kuloŵa m'nyumba ya munthu wamphamvu nkufunkha chuma chake, atapanda kuyamba wamumanga munthu wamphamvuyo. Atatero ndiye angafunkhe zam'nyumbamo. “Munthu wosavomerezana ndi Ine, ndiye kuti ndi wotsutsana nane. Ndipo wosandithandiza kusonkhanitsa, ndiye kuti ameneyo ndi womwaza. Nchifukwa chake ndikunenetsa kuti Mulungu adzakhululukira anthu tchimo lililonse, ngakhale mau achipongwe omunyoza Iyeyo. Koma munthu wochita chipongwe Mzimu Woyera, Mulungu sadzamkhululukira. Chimodzimodzinso aliyense wonenera zoipa Mwana wa Munthu, Mulungu adzamkhululukira. Koma aliyense wonenera zoipa Mzimu Woyera, Mulungu sadzamkhululukira konse nthaŵi ino, ngakhalenso nthaŵi ilikudza.” “Mukanena kuti, ‘Mtengo uwu ngwabwino,’ ndiye kuti zipatso zakenso nzabwino. Koma mukanena kuti, ‘Mtengo uwu ngwoipa,’ ndiye kuti zipatso zakenso nzoipa. Pajatu mtengo umadziŵika ndi zipatso zake. Ana a njoka inu, mungathe bwanji kulankhula zabwino pamene muli oipa? Pajatu pakamwa pamalankhula zimene zadzaza mu mtima. Munthu wabwino amatulutsa zabwino m'chuma chabwino cha mumtima mwake. Nayenso munthu woipa amatulutsa zoipa m'chuma choipa cha mumtima mwake. Ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo, anthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mau aliwonse opanda pake amene adaalankhula. Mwakuti chifukwa cha mau ako omwe mlandu udzakukomera kapena kukuipira.” Pamenepo aphunzitsi ena a Malamulo ndi Afarisi ena adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, tifuna kuti mutiwonetse chizindikiro chozizwitsa.” Koma Yesu adati, “Anthu a mbadwo uno ndi oipa ndi osakhulupirika, amafuna kuwona chizindikiro chozizwitsa. Komabe sadzachiwona chizindikirocho, kupatula cha mneneri Yona chija. Monga Yona uja anali m'mimba mwa chinsomba chija masiku atatu, usana ndi usiku, chomwechonso Mwana wa Munthu adzakhala m'kati mwa nthaka masiku atatu, usana ndi usiku. Pa tsiku la chiweruzo anthu a ku Ninive adzauka pamodzi ndi anthu a mbadwo uno, nadzaŵatsutsa. Paja iwowo adaatembenuka mtima, atamva malaliko a Yona. Ndipotu pano pali woposa Yona amene. Pa tsiku la chiweruzo mfumukazi yakumwera ija idzauka pamodzi ndi anthu a mbadwo uno nidzaŵatsutsa. Paja iyo idaachita kuchokera ku mathero a dziko lapansi kudzamva zolankhula zanzeru za mfumu Solomoni. Ndipotu pano pali woposa Solomoni amene.” “Mzimu woipa ukatuluka mwa munthu, umakayendayenda ku malo opanda madzi, kufunafuna malo opumulirako, koma osaŵapeza. Ndiye umati, ‘Ndibwerera kunyumba kwanga komwe ndidatuluka kuja.’ Tsono ukafika, umapeza m'nyumba muja muli zii, mosesasesa ndi mokonza bwino. Pamenepo umakatenga mizimu ina isanu ndi iŵiri yoipa koposa uwowo, kenaka yonseyo imaloŵa nkukhazikika momwemo. Choncho mkhalidwe wotsiriza wa munthu uja umaipa koposa mkhalidwe wake woyamba. Zidzateronso ndi anthu ochimwa amakono.” Pamene Yesu ankalankhula ndi anthu ambirimbiri aja, nthaŵi yomweyo amai ake ndi abale ake adafika, naima panja. Ankafuna mpata woti alankhule naye. Tsono munthu wina adauza Yesu kuti, “Amai anu ndi abale anu ali panjapa, akufuna kulankhula nanu.” Yesu adamuyankha kuti, “Kodi ine amai anga ndani? Ndipo abale anga ndani?” Atatero, adaloza ophunzira ake nati, “Inetu amai anga ndi abale anga ndi aŵa. Pakuti aliyense wochita zimene Atate anga akumwamba akufuna, ameneyo ndiye mbale wanga ndi mlongo wanga ndi amai anga.” Tsiku lomwelo Yesu adatuluka m'nyumba nakakhala pansi m'mbali mwa nyanja. Anthu ambirimbiri adasonkhana kumene kunali Iye. Tsono Yesu adaloŵa m'chombo nakhala pansi, anthu onse aja ataima pa mtunda. Yesu adalankhula nawo zambiri m'mafanizo. Adati, “Munthu wina adaapita kukafesa mbeu. Akufesa choncho, mbeu zina zidagwera m'njira, ndipo mbalame zidabwera nkuzitolatola. Mbeu zina zidagwera pa nthaka yamiyala, pamene panalibe dothi lambiri. Zidamera msanga chifukwa nthakayo inali yosazama. Koma pamene dzuŵa lidakwera, zidapserera kenaka zidauma, chifukwa zinali zosazika mizu. Mbeu zina zidagwera pa zitsamba zaminga. Zitsambazo pokula zidalanda chakudya cha mbeu zija. Koma mbeu zina zidagwera pa nthaka yabwino, ndipo zidabereka. Ngala zina zinali ndi njere makumi khumi, zina makumi asanu ndi limodzi, zina makumi atatu.” Tsono Yesu adati, “Amene ali ndi makutu, amve!” Pambuyo pake ophunzira a Yesu aja adadzamufunsa kuti, “Kodi bwanji anthuŵa mumalankhula nawo m'mafanizo?” Iye adati, “Inuyo Mulungu adakuululirani zobisika zokhudza Ufumu wakumwamba. Koma enaŵa sadaŵaululire ai. Pajatu amene ali nkanthu kale, adzampatsanso zina, nadzakhala ndi zochuluka. Koma amene alibe kanthu, adzamlanda ngakhale kakang'onong'ono kamene ali nako. Tsono anthuŵa ndimalankhula nawo m'mafanizo, chifukwa ngakhale amapenya, komabe saona, ndipo ngakhale amamva, komabe samva kwenikweni kapena kumvetsa. Ndi iwoŵa zikuchitikadi zimene mneneri Yesaya adaanena kuti, “ ‘Kumva mudzamva ndithu, koma osamvetsa, kuyang'ana mudzayang'ana ndithu, koma osapenya. Ndithu anthu ameneŵa nzeru zao nzobuntha, adagonthetsa makutu ao, ndipo adapsinya maso ao, kuwopa kuti angamapenye ndi maso aowo, angamamve ndi makutu aowo, angamamvetse ndi nzeru zaozo, ndi kutembenuka mtima, Ineyo nkuŵachiritsa.’ “Koma inu ndinu odala, popeza kuti maso anu akupenya, ndipo makutu anu akumva. Kunena zoona aneneri ambiri ndi anthu ambiri olungama, adaafunitsitsa kuwona zimene inu mukupenyazi, koma sadaziwone. Adaafunitsitsa kumva zimene inu mukumvazi, koma sadazimve.” “Tsono inu mumvetse bwino tanthauzo lake la fanizo la munthu wofesa mbeu lija. Munthu aliyense akamva mau onena za Ufumu wakumwamba, koma osaŵamvetsa, Woipa uja amabwera nkudzalanda zimene zidafesedwa mumtima mwake. Zimenezi ndiye mbeu zogwera m'njira zija. Mbeu zofesedwa pa nthaka yamiyala zija zikutanthauza munthu amene amamva mau a Mulungu, nthaŵi yomweyo nkuŵalandira ndi chimwemwe. Tsono popeza kuti alibe mizu yozama, amangolimbika kanthaŵi pang'ono chabe. Mwakuti pakangofika mavuto kapena masautso chifukwa cha mau aja, nthaŵi yomweyo munthuyo amabwerera m'mbuyo. Mbeu zofesedwa pa zitsamba za minga zija zikutanthauza munthu amene amamva mau a Mulungu. Koma kutanganidwa ndi za pansi pano ndi kukondetsa chuma kumafooketsa mau aja, motero sabereka konse zipatso. Koma mbeu zofesedwa pa nthaka yabwino zija zikutanthauza munthu amene amamva mau a Mulungu naŵamvetsa. Munthu wotere amaberekadi zipatso, mwina makumi khumi, mwina makumi asanu ndi limodzi, mwina makumi atatu.” Yesu adaŵaphera fanizo linanso. Adati, “Za Ufumu wakumwamba tingazifanizire motere: Munthu wina adaafesa mbeu zabwino m'munda mwake. Koma anthu onse ali m'tulo, mdani wake adabwera, nkufesa namsongole pakati pa tirigu, nachokapo. Tsono pamene mmera udakula nkuyamba kuchita njere, namsongole uja nayenso adayamba kuwoneka. Antchito a mwinimunda uja adadzamufunsa kuti, ‘Bwana, kodi suja mudaafesa mbeu zabwino m'munda mwanu? Nanga bwanji mukuwonekanso namsongole?’ Iye adaŵayankha kuti, ‘Ndi mdani amene wachita zimenezi.’ Antchito aja adamufunsa kuti, ‘Bwanji tikamzule?’ Koma iye adati, ‘Iyai, mungakazulire kumodzi ndi tirigu pozula namsongoleyo. Zilekeni zikulire pamodzi zonse mpaka nyengo yodula. Pa nthaŵi imeneyo ndidzauza odula kuti, Yambani mwazula namsongole, mummange m'mitolo kuti mukamtenthe. Kenaka musonkhanitse tirigu ndi kukamthira m'nkhokwe yanga.’ ” Yesu adaŵaphera fanizo linanso. Adati, “Ufumu wakumwamba uli ngati njere ya mbeu ya mpiru imene munthu adakaifesa m'munda mwake. Ndi yaing'ono kwambiri mukaiyerekeza ndi njere zina zonse. Komabe mbeu yake ikakula, imapambana zitsamba zina zonse. Imasanduka mtengo, mbalame zamumlengalenga nkumabwera kudzamanga zisa pa nthambi zake.” Yesu adaŵaphera fanizo linanso. Adati, “Ufumu wakumwamba ulinso ngati chofufumitsira buledi, chimene mai wina adachisanganiza ndi ufa wokwanira miyeso itatu, mpaka mtanda wonse udafufuma.” Zonsezi Yesu adalankhula ndi anthu aja m'mafanizo. Sadalankhule nawo kanthu popanda fanizo. Zidaatero kuti zipherezere zimene mneneri adaanena kuti, “Ndidzalankhula nawo m'mafanizo. Ndidzaulula zimene zinali zobisika chilengedwere dziko lapansi.” Pambuyo pake Yesu adaŵasiya anthu ambirimbiri aja, nakaloŵa m'nyumba. Tsono ophunzira ake adadzampempha kuti, “Tatimasulirani fanizo la namsongole wam'munda lija.” Yesu adati, “Wofesa mbeu zabwino uja ndi Mwana wa Munthu. Munda uja ndi dziko lino lapansi. Mbeu zabwino zija ndi anthu ake a Ufumu wakumwamba. Namsongole uja ndi anthu ake a Woipa uja. Mdani wodzafesa namsongole uja ndi Satana. Kudula kuja nkutha kwake kwa dziko lino lapansi, ndipo odula aja ndi angelo. Monga momwe adaazulira namsongole uja nkumutentha pa moto, zidzateronso pa kutha kwa dziko lino lapansi. Mwana wa Munthu adzatuma angelo ake kudzachotsa mu Ufumu wake anthu onse ochimwitsa anzao, ndi ena onse ochita zoipa, nadzaŵaponya m'ng'anjo ya moto. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano. Tsono anthu olungama adzaŵala ngati dzuŵa mu Ufumu wa Atate ao. Amene ali ndi makutu, amve! “Ufumu wakumwamba uli ngati chuma chobisika m'munda. Munthu wina atachitumba, amachibisanso. Kenaka mokondwa amakagulitsa zonse zimene ali nazo, nkukagula munda uja. “Ndiponso Ufumu wakumwamba uli ngati munthu wamalonda wonka nafunafuna ngale zokongola zamtengowapatali. Atapeza ngale imodzi yamtengowapatali kwambiri, amakagulitsa zonse zimene ali nazo, nkukagula ngale ija. “Ufumu wakumwamba ulinso ngati khoka limene anthu amaliponya m'nyanja, ndipo limagwira nsomba za mitundu yonse. Likadzaza, anthu amalikokera ku mtunda. Tsono amakhala pansi, nsomba zabwino nkumaziika m'madengu, zachabe nkumangozitaya. Zidzateronso pa kutha kwa dziko lino lapansi. Angelo adzabwera nadzachotsa anthu ochimwa pakati pa anthu olungama, nkumaŵaponya m'ng'anjo ya moto. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.” Yesu adaŵafunsa anthu aja kuti, “Mwazimvetsa zonsezi kodi?” Iwo adati, “Inde.” Apo Iye adaŵauza kuti, “Nchifukwa chaketu mphunzitsi aliyense wa Malamulo, amene adaphunzira za Ufumu wakumwamba, ali ngati mwinibanja amene amatulutsa zinthu zatsopano ndi zinthu zakale m'nkhokwe ya chuma chake.” Yesu atatsiriza kunena mafanizoŵa, adachoka kumeneko. Atafika ku dera lakwao, adayamba kuphunzitsa anthu m'nyumba yao yamapemphero. Amene ankamumva ankadabwa nkumati, “Kodi Iyeyu, nzeru zimenezi ndi mphamvuzi adazitenga kuti? Kodi ameneyu si mwana wa mmisiri wa matabwa uja? Kodi suja mai wake ndi Maria? Ndipo abale ake si Yakobe, Yosefe, Simoni ndi Yuda? Kodi suja alongo ake onse ali nafe pompano? Nanga tsono zonsezi adazitenga kuti?” Choncho adakhumudwa naye. Koma Yesu adaŵauza kuti, “Mneneri amalemekezeka kwina kulikonse, kupatula kumudzi kwao ndiponso kubanja kwao.” Motero sadachite zamphamvu zambiri kumeneko, chifukwa cha kusakhulupirira kwa anthuwo. Pa nthaŵi imeneyo Herode, mfumu ya ku Galileya, adaamva zimene anthu ankanena za Yesu. Tsono adauza nduna zake kuti, “Ameneyu ndi Yohane Mbatizi uja, adauka kwa akufa, nkuwona akuchita zamphamvu zonsezi.” Pajatu Herode kale adaatuma asilikali ake kuti akagwire Yohane, akammange ndi kumponya m'ndende. Adaachita zimenezi chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa Filipo, mbale wake. Pakuti Yohane adaauza Herode kuti, “Nkulakwira Malamulo kumukwatira mkaziyo.” Kwenikweni Herode ankafuna kupha Yohane, koma ankaopa anthu, chifukwa iwo ankati ndi mneneri. Pa tsiku lokumbukira kubadwa kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodiasi adaavina pamaso pa anthu oitanidwa ku phwando, mwakuti adaakondwetsa Herode kwambiri. Motero Herode adaalonjeza molumbira kuti, “Ndithudi, ndidzakupatsa chilichonse chimene ungapemphe.” Tsono mai wake atamuuza choti apemphe, mwana wamkazi uja adati, “Mundipatse pompano mutu wa Yohane Mbatizi m'mbale.” Pamenepo mfumu Herode adamva chisoni. Koma chifukwa cha malumbiro ake ndiponso chifukwa cha anthu oitanidwa ku phwando aja, adalamula kuti ampatse mutu adaapemphawo. Tsono adatuma munthu kuti akamdule mutu Yohaneyo m'ndende. Mutuwo adautengera m'mbale nakaupereka kwa mtsikana uja, mtsikanayo nkukaupereka kwa mai wake. Pambuyo pake ophunzira a Yohane adabwera nadzatenga mtembo wake nkukauika m'manda. Kenaka adapita kukauza Yesu. Yesu atazimva zimenezi, adachokako kumeneko m'chombo, kuti apite kwayekha kwazii. Koma anthu atamva, adayenda pa mtunda namlondola kuchokera ku mizinda yao. Yesu adatuluka m'chombomo, ndipo pamene adaŵaona anthu ambirimbiriwo, adaŵamvera chifundo, nayamba kuchiritsa amene ankadwala. Nthaŵi yamadzulo ophunzira ake adadzamuuza kuti, “Kunotu nkuthengo, ndipo ano ndi madzulo. Auzeni anthuŵa azinyamuka, apite ku midzi kuti azikagula chakudya.” Koma Yesu adaŵauza kuti, “Palibe chifukwa choti achokere. Inuyo apatseni chakudya.” Iwo adati, “Pano tili ndi buledi msanu yekha ndi nsomba ziŵiri, basi.” Yesu adati, “Bwera nazoni kuno.” Atatero, adalamula kuti anthu aja akhale pansi pa udzu. Tsono adatenga buledi msanu uja ndi nsomba ziŵiri zija, nayang'ana kumwamba, nkuthokoza Mulungu. Kenaka atanyemanyema bulediyo, adazipereka kwa ophunzira ake, ophunzira aja nkukagaŵira anthuwo. Anthu onsewo adadya mpaka kukhuta. Pambuyo pake ophunzira aja adatola zotsala nkudzaza madengu khumi ndi aŵiri. Koma tsono anthu amene adaadyawo analipo ngati zikwi zisanu amuna okha, osaŵerenga akazi ndi ana. Madzulo omwewo Yesu adalamula ophunzira ake kuti aloŵe m'chombo, atsogole kupita ku tsidya, pamene Iye akuuza anthu kuti azipita kwao. Tsono atatsazikana nawo anthu aja, Iye adakwera ku phiri yekha kukapemphera. M'mene kunkayamba kuda, nkuti ali komweko yekhayekha. Pamenepo nkuti chombo chija chili kutalitali ndi mtunda, chikuvutika ndi mafunde, chifukwa chinali chitayang'anana ndi mphepo. M'mamaŵa kukali mbuu, Yesu adadza kwa iwo Iye akuyenda pa madzi. Pamene ophunzira aja adamuwona akuyenda pa madzi, adaopsedwa nati, “Ndi mzukwa!” Ndipo adayamba kukuwa chifukwa cha mantha. Koma nthaŵi yomweyo Yesu adaŵauza kuti, “Khazikani mtima pansi, ndine; musaope.” Apo Petro adati, “Ambuye, ngati ndinudi, tandiwuzani kuti ndibwere kwa Inu pamadzipo.” Yesu adati, “Chabwino, bwera.” Tsono Petro adatuluka m'chombo nayamba kuyenda pa madzi kupita kwa Yesu. Koma ataona m'mene ikuwombera mphepo, adachita mantha, nkuyamba kumira. Tsono adafuula kuti, “Ambuye, pulumutseni!” Pompo Yesu adatambalitsa dzanja nkumugwira nati, “Iwe wa chikhulupiriro chochepawe, unakayikiranji?” Pambuyo pake aŵiriwo adaloŵa m'chombo muja, mphepo nkuleka. Apo amene anali m'chombo aja adamgwadira Yesu nati, “Ndithudi, ndinu Mwana wa Mulungu.” Tsono onse adaoloka nyanja nakafika ku Genesarete. Anthu akumeneko adamzindikira Yesu, nakadziŵitsa anzao a ku dera lonse lozungulira pamenepo. Motero adadza kwa Yesu ndi anthu onse odwala. Adampempha kuti aŵalole odwalawo kungokhudza ngakhale mphonje ya chovala chake. Mwakuti onse amene ankaikhudza, ankachira. Tsiku lina Afarisi ena ndi aphunzitsi ena a Malamulo adadza kwa Yesu kuchokera ku Yerusalemu. Adamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani ophunzira anu sasunga mwambo wa makolo? Sasamba m'manja moyenera akamadya chakudya.” Yesu adaŵayankha kuti, “Nanga bwanji inuyo, chifukwa choumirira miyambo yanu, mumaphwanya lamulo la Mulungu? Paja Mulungu adalamula kuti, ‘Lemekeza atate ako ndi amai ako,’ ndiponso kuti, ‘Wonyoza atate ake kapena amai ake, aziphedwa basi.’ Koma inu mumati, ‘Munthu akauza atate ake kapena amai ake kuti, “Zimene ndikadakuthandiza nazoni, ndazipereka kwa Mulungu,” ameneyo sasoŵanso kulemekeza atate ake.’ Pakutero, chifukwa cha mwambo wanuwo, mau a Mulungu inu mumaŵasandutsa achabechabe. Inu anthu achiphamaso, ndithu mneneri Yesaya adaanenadi zoona muja adaati, “ ‘Anthu aŵa amangondilemekeza ndi pakamwa chabe, koma mtima wao uli kutali ndi Ine. Amandipembedza inde, koma kupembedza kwaoko nkopanda phindu, chifukwa zimene amaphunzitsa ngati zophunzitsa zenizeni ndi malamulo a anthu chabe.’ ” Pambuyo pake Yesu adaitana anthu aja kuti adze pafupi, ndipo adaŵauza kuti, “Mverani ndipo mumvetse bwino. Si chinthu choloŵa m'kamwa mwa munthu chimene chimamuipitsa ai, koma chotuluka m'kamwa mwake ndiye chimene chimamuipitsa.” Pamenepo ophunzira ake adadzamufunsa kuti, “Kodi mukudziŵa kuti Afarisi aja akhumudwa atamva zija mwanenazi?” Yesu adati, “Chomera chilichonse chimene sichidabzalidwe ndi Atate anga akumwamba, chidzazulidwa. Alekeni, ndi atsogoleri akhungu ameneŵa. Tsono ngati wakhungu atsogolera wakhungu mnzake, onse aŵiri adzagwa m'dzenje.” Apo Petro adampempha kuti, “Timasulirenitu fanizoli.” Yesu adati, “Kani ngakhale inunso simumvetsa? Kodi inu simuzindikira kuti zonse zoloŵa m'kamwa mwa munthu zimaloŵa m'mimba mwake, pambuyo pake nkukatayidwa kuthengo? Koma zotuluka m'kamwa mwa munthu zimachokera mu mtima, ndipo zimenezi ndizo zimamuipitsa. Chifukwa m'kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, za kuphana, za chigololo, za chiwerewere, za kuba, maumboni onama, ndiponso zachipongwe. Zimenezi ndizo zimaipitsa munthu. Koma kudya chakudya osasamba m'manja, sikungaipitse munthu.” Yesu adachoka kumeneko, napita ku madera a ku Tiro ndi Sidoni. Mai wina wachikanani, wa ku madera amenewo, adadza kwa Yesu. Adafuula kuti, “Mundichitire chifundo, Inu Ambuye, Mwana wa Davide. Mwana wanga wamkazi ngwogwidwa koopsa ndi mzimu woipa.” Koma Yesu sadamuyankhe mau ndi amodzi omwe. Ophunzira ake adadza nampempha kuti, “Muuzeni azipita, onani akubwera natisokosera.” Yesu adati, “Inetu Mulungu adandituma kwa amene ali ngati nkhosa zotayika pa mtundu wa Aisraele.” Mai uja adadzamgwadira nati, “Ambuye, ndithu thandizeni.” Yesu adamuuza kuti, “Sibwino kutenga chakudya cha ana nkuponyera agalu.” Maiyo adati, “Nzoonadi, Ambuye, koma suja ngakhale agalu omwe amadyako nyenyeswa zimene zimagwa pansi kuchokera pa tebulo la mbuye ao?” Apo Yesu adati, “Inu mai, chikhulupiriro chanu nchachikulu. Zichitikedi zimene mukufuna.” Pompo mwana wake wamkazi uja adachira. Pambuyo pake Yesu adachoka kumeneko, nayenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya. Kenaka adakwera m'phiri nakakhala pansi kumeneko. Anthu ambirimbiri adadza kwa Iye ndi anthu opunduka miyendo, akhungu, olumala, osalankhula, ndiponso ndi odwala ena ambiri. Adaŵakhazika pafupi ndi Yesu, Iye nkuŵachiritsa. Tsono anthu onse adadabwa poona kuti osalankhula aja akulankhula, olumala aja achira, opunduka miyendo aja akuyenda, ndipo akhungu aja akupenya. Choncho adatamanda Mulungu wa Israele. Yesu adaitana ophunzira ake, naŵauza kuti, “Ndikuŵamvera chifundo anthuŵa, chifukwa akhala nane masiku atatu tsopano, ndipo alibe chakudya. Sindifuna kuŵabweza kwao ali ndi njala chonchi, kuwopa kuti angalefuke pa njira.” Ophunzirawo adamufunsa kuti, “Anthu ochuluka chotereŵa tingaŵapezere kuti chakudya chokwanira, kuthengo ngati kuno?” Yesu adaŵafunsa kuti, “Kaya buledi muli naye mngati?” Iwo aja adati, “Msanu ndi muŵiri, ndiponso tinsomba toŵerengeka.” Apo Yesu adalamula anthu aja kuti akhale pansi. Kenaka adatenga buledi msanu ndi muŵiri uja, ndi nsomba zija, adathokoza Mulungu, nazinyemanyema nkuzipereka kwa ophunzira ake, iwowo nakazigaŵira anthu aja. Anthu onsewo adadya mpaka kukhuta. Adatola zotsala, nkudzaza madengu asanu ndi aŵiri. Koma tsono anthu amene adaadyawo, analipo zikwi zinai amuna okha, osaŵerenga akazi ndi ana. Pambuyo pake Yesu adatsazikana nawo anthu aja, kenaka Iye adaloŵa m'chombo napita ku dera la Magadani. Tsiku lina kudabwera Afarisi ndi Asaduki ena kwa Yesu. Adampempha kuti aŵaonetse chizindikiro chozizwitsa chochokera kumwamba. Pakutero ankangofuna kumutchera msampha. Koma Yesu adaŵauza kuti, “Pamene dzuŵa likuloŵa, mumati, ‘Maŵa kucha bwino, popeza kuti kumwamba kuli psuu.’ Ndipo m'maŵa mumati, ‘Lero ndiye kugwa mvula yamkuntho, popeza kuti kumwambaku kwachita mitambo yabii.’ Mumatha kutanthauzira m'mene kukuwonekera kumwambaku, koma osatha kutanthauzira zizindikiro za nthaŵi zino. Anthu a mbadwo woipa ndi wosakhulupirika amafuna kuwona chizindikiro chozizwitsa. Komabe sadzaona chizindikiro china kupatula chokha chija cha mneneri Yona.” Atatero, Yesu adaŵasiya nachokapo. Pamene ophunzira aja adakafika kutsidya, anali ataiŵala kutenga buledi. Yesu adaŵauza kuti, “Muchenjere nacho chofufumitsira buledi cha Afarisi ndi Asaduki.” Apo ophunzirawo adayamba kukambirana nkumati, “Akuterotu chifukwa sitidatenge buledi.” Yesu adaadziŵa zimene iwo ankanena. Ndiye adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukukambirana zakuti mulibe buledi, inu a chikhulupiriro chochepanu? Kodi mpaka pano simunamvetsebe? Kodi simukukumbukira kuti ndi buledi msanu ndidadyetsa anthu zikwi zisanu? Nanga mudaadzaza madengu angati ndi zotsala? Sujanso ndi buledi msanu ndi muŵiri ndidadyetsa anthu zikwi zinai? Nanga mudaadzaza madengu angati a zotsala? Nanga bwanji simukuzindikira kuti sindimanena za buledi? Chenjera nachoni chofufumitsira buledi cha Afarisi ndi Asaduki.” Pamenepo iwo adazindikira kuti Yesu sankaŵauza kuti achenjere ndi chofufumitsira buledi, koma kuti achenjere ndi zophunzitsa za Afarisi ndi Asaduki. Pamene Yesu adafika ku madera a ku Kesareya-Filipi, adafunsa ophunzira ake kuti, “Kodi anthu amati Mwana wa Munthune ndine yani?” Iwo adati, “Ena amati ndinu Yohane Mbatizi, ena amati ndinu Eliya, enanso amati ndinu Yeremiya kapena mmodzi mwa aneneri.” Apo Yesu adaŵafunsa kuti, “Nanga inuyo, mumati ndine yani?” Simoni Petro adayankha kuti, “Inu ndinu Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu wamoyo.” Yesu adamuuza kuti, “Ndiwe wodala, Simoni mwana wa Yona, pakuti si munthu wakuululira zimenezi ai, koma ndi Atate anga amene ali Kumwamba. Ndipo Ine ndikuti, Ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe limeneli ndidzamanga Mpingo wanga. Ndipo ngakhale mphamvu za imfa sizidzaugonjetsa. Ndidzakupatsa makiyi a Ufumu wakumwamba, kotero kuti zimene udzamange pansi pano, zidzamangidwa ndi Kumwamba komwe, ndipo zimene udzamasule pansi pano, zidzamasulidwa ndi Kumwamba komwe.” Yesu atanena zimenezi, adalamula ophunzira aja kuti asauze munthu aliyense kuti Iye ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja. Kuyambira nthaŵi imeneyo Yesu adayamba kudziŵitsa ophunzira ake kuti, “Ndiyenera kupita ku Yerusalemu, kumeneko akulu a Ayuda ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo adzandizunza kwambiri. Ndidzaphedwa koma mkucha wake ndidzauka.” Apo Petro adamtengera pambali nayamba kumdzudzula. Adati, “Pepani Ambuye, zisatero ai. Mulungu asalole zimenezi.” Koma Yesu adacheuka namdzudzula. Adati, “Choka apa, iwe Satana! Ufuna kundilakwitsa. Maganizo akoŵa si maganizo a Mulungu ai, ndi maganizo a anthu chabe.” Atatero Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Munthu wofuna kutsata Ine, adzikane mwiniwakeyo, ndipo asenze mtanda wake nkumanditsata. Chifukwa wofuna kupulumutsa moyo wake, adzautaya, koma wotaya moyo wake chifukwa cha Ine, adzaupeza. Nanga ndiye kuti munthu angapindulenji atapata zonse zapansipano, iyeyo nkutaya moyo wake? Munthu angalipire chiyani choti aombolere moyo wake? Ndipotu Mwana wa Munthu adzabwera ndi angelo ake ali ndi ulemerero wa Atate ake. Pamenepo adzabwezera aliyense molingana ndi zochita zake. Ndithu ndikunenetsa kuti alipo ena pompano omwe sadzafa asanaone Mwana wa Munthu akubwera ndi ulemerero waufumu.” Patapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu adatenga Petro, Yakobe ndi Yohane, mbale wa Yakobeyo, nakwera nawo ku phiri lalitali, kwaokha. Tsono maonekedwe a Yesu adasinthika iwo akuwona. Nkhope yake idaŵala ngati dzuŵa, ndipo zovala zake zidachita kuti mbee kuyera. Nthaŵi yomweyo ophunzira aja adaona Mose ndi Eliya akulankhula naye. Petro adauza Yesu kuti, “Ambuye, ndi bwino kuti ife tili nao pano. Ngati mukufuna, ndimanga misasa itatu pano, wina wanu, wina wa Mose, wina wa Eliya.” Akulankhula choncho, kudadza mtambo woŵala nuŵaphimba. Mumtambomo mudamveka mau akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimamkonda, ndipo ndimakondwera naye kwambiri. Muzimumvera.” Ophunzira aja atamva zimenezi, adachita mantha kwambiri nadzigwetsa chafufumimba. Koma Yesu adabwera, naŵakhudza nkunena kuti, “Dzukani, musachite mantha.” Iwo aja poŵeramuka, adangoona kuti palibe munthu winanso, koma Yesu yekha. Pamene ankatsika phiri lija, Yesu adaŵalamula kuti, “Zimene mwaona m'masomphenyazi musakauze wina aliyense mpaka Mwana wa Munthu atauka kwa akufa.” Ophunzira aja adamufunsa kuti, “Nanga bwanji aphunzitsi a Malamulo amati Eliya adzayenera kuyamba wabwera?” Yesu adati, “Inde Eliya ayambadi wabwera nkudzakonzanso zonse. Koma ndikunenetsa kuti Eliya adabwera kale, ndipo anthu sadamzindikire, koma adamchita zonse zimene iwo ankafuna. Chonchonso Mwana wa Munthu adzazunzidwa ndi anthuwo.” Pamenepo ophunzira aja adazindikira kuti ankaŵauza za Yohane Mbatizi. Pamene iwo adafikanso kumene kunali khamu la anthu kuja, munthu wina adadzagwadira Yesu. Adati, “Ambuye mchitireni chifundo mwana wanga. Ali ndi khunyu ndipo amavutika koopsa. Kaŵirikaŵiri amagwa pa moto mwinanso m'madzi. Ndinabwera naye kwa ophunzira anuŵa, koma alephera kumchiritsa.” Yesu adati, “Ha! Anthu a m'badwo wopanda chikhulupiriro ndi wopotoka maganizo! Ndiyenera kukhala nanube mpaka liti? Ndiyenera kukupirirani mpaka liti? Tabwera nayeni kuno mwanayo.” Atatero, Yesu adazazira mzimu woipawo, ndipo udatuluka mwa mnyamatayo. Pompo iye adachira. Pambuyo pake ophunzira aja adadza kwa Yesu paseri namufunsa kuti, “Ifeyo ndiye tinalephera bwanji kuutulutsa mzimu woipa uja?” Yesu adaŵayankha kuti, “Chifukwa chake nchakuti chikhulupiriro chanu nchochepa. Ndithu ndikunenetsa kuti mutakhala ndi chikhulupiriro ngakhale chochepa ngati kambeu ka mpiru, mudzauza phiri ili kuti, ‘Choka apa, pita uko,’ ilo nkuchokadi. Mwakuti palibe kanthu kamene kadzakukanikeni.” [ “Koma mzimu wa mtundu umenewu, pokhapokha mutayamba mwapemphera ndi kusala zakudya mpamene mungautulutse.”] Tsiku lina ophunzira atasonkhana onse ku Galileya, Yesu adaŵauza kuti, “Mwana wa Munthu akudzaperekedwa kwa anthu. Iwo adzamupha, koma mkucha wake Iye adzauka.” Ophunzirawo atamva zimenezi, adagwidwa ndi chisoni chachikulu. Pamene Yesu ndi ophunzira ake adafika ku Kapernao, okhometsa msonkho wa ku Nyumba ya Mulungu adadzafunsa Petro kuti, “Kodi aphunzitsi anuŵa sakhoma msonkho wa ku Nyumba ya Mulungu?” Iye adati, “Amakhoma.” Tsono Petro ataloŵa m'nyumba, asananene chilichonse, Yesu adamufunsa kuti, “Iwe Simoni, ukuganiza bwanji? Kodi mafumu apansipano amalandira msonkho kwa yani? Kwa anthu a mtundu wao, kapena kwa alendo?” Petro adati, “Kwa alendo.” Apo Yesu adamuuza kuti, “Tsono ndiye kutitu anthu a mtundu wao sayenera kukhoma. Koma kuwopa kuŵakhumudwitsa a ku Nyumba ya Mulunguŵa, kaŵedze nsomba ku nyanja. Nsomba imene ukayambire kuŵedza, ukaikanule kukamwa, ndipo ukapezamo ndalama. Ukatenge ndalamayo nkukakhomera msonkho wanga ndi wako womwe.” Nthaŵi yomweyo ophunzira aja adadzamufunsa Yesu kuti, “Kodi mu Ufumu wakumwamba wamkulu koposa onse ndani?” Apo Yesu adaitana mwana namuimiritsa pakati pao, ndipo adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti mukapanda kusintha ndi kusanduka ngati ana, simudzaloŵa konse mu Ufumu wakumwamba. Nchifukwa chake munthu wodzichepetsa ngati mwana uyu, ameneyo ndiye wamkulu mu Ufumu wakumwamba. Ndipo aliyense wolandira bwino mwana wonga ngati uyu chifukwa cha Ine, ndiye kuti akulandira bwino Ine amene.” “Aliyense wochimwitsa ngakhale mmodzi mwa ana okhulupirira Ineŵa, ameneyo kukadakhala kwabwino koposa kuti ammangirire chimwala cha mphero m'khosi ndi kukammiza m'nyanja pozama. Ali ndi tsoka anthu apansipano chifukwa cha zochimwitsa. Zochimwitsazo sizingalephere kuwoneka, koma ali ndi tsoka munthu wobweretsa zochimwitsayo. “Tsono ngati dzanja lako kapena phazi lako likuchimwitsa, lidule ndi kulitaya. Ndi bwino kuti ukaloŵe ku moyo uli woduka dzanja kapena phazi, kupambana kuti ukaponyedwe ku moto wosatha uli ndi manja onse kapena mapazi onse aŵiri. Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, likolowole ndi kulitaya. Ndi bwino kuti ukaloŵe ku moyo uli ndi diso limodzi lokha, kupambana kuti ukaponyedwe ku moto wa Gehena uli ndi maso aŵiri.” “Chenjerani kuti musanyoze ndi mmodzi yemwe mwa anaŵa. Ndithu ndikunenetsa kuti angelo ao Kumwamba amakhala pamaso pa Atate anga amene ali Kumwambako nthaŵi zonse.” [ “Pajatu Mwana wa Munthu adabwera kudzapulumutsa amene adatayika.”] “Tsono mukuganiza bwanji? Munthu atakhala ndi nkhosa 100, imodzi nkutayika, kodi sangasiye 99 zina zija m'phiri nkukafunafuna imodzi yotayikayo? Ndithu ndikunenetsa kuti ataipeza, chimwemwe chake chokondwerera imeneyo chimapambana chokondwerera zina zija zimene sizidatayike. Chonchonso Atate anu amene ali Kumwamba safuna kuti ndi mmodzi yemwe mwa anaŵa atayike. “Mbale wako akakuchimwira, pita ukamdzudzule muli aŵiri nokha. Akakumvera, wamkonza mbale wakoyo. Koma akapanda kukumvera, utengerepo wina mmodzi kapena ena aŵiri, kuti mau onse akatsimikizike ndi mboni ziŵiri kapena zitatu. Akapanda kuŵamvera iwowo, ukauze Mpingo. Ndipo akapanda kumveranso ndi Mpingo womwe, umuyese munthu wakunja kapena wokhometsa msonkho. “Ndithu ndikunenetsa kuti chilichonse chimene mudzamanga pansi pano, chidzamangidwa ndi Kumwamba komwe, ndipo chilichonse chimene mudzamasula pansi pano, chidzamasulidwa ndi Kumwamba komwe. “Ndikunenetsanso kuti aŵiri mwa inu mutavomerezana pansi pano popempha kanthu kalikonse, Atate anga akumwamba adzakupatsani. Pajatu pamene aŵiri kapena atatu asonkhana m'dzina langa, Ineyo ndili nao pomwepo.” Pamenepo Petro adadzafunsa Yesu kuti, “Ambuye, kodi mbale wanga atamandichimwira, ndidzamkhululukire kangati? Kodi ndidzachite kufikitsa kasanunkaŵiri?” Yesu adamuyankha kuti, “Kodi ndikuti kasanunkaŵiri kokha ngati, iyai, koma mpaka kasanunkaŵiri kuchulukitsa ndi makumi asanu ndi aŵiri. “Tsono Ufumu wakumwamba tingaufanizire motere: Panali mfumu ina imene idaaitanitsa antchito ake kuti iwonenso bwino ngongole zao. Atangoyamba kumene, adabwera ndi wantchito wina amene anali ndi ngongole ya ndalama zochuluka kwabasi. Ndiye popeza kuti adaasoŵa chobwezera ngongoleyo, mbuye wake uja adalamula kuti amgulitse wantchitoyo pamodzi ndi mkazi wake ndi ana ake ndi zake zonse, kuti ngongole ija ibwezedwe. Apo wantchito uja adamgwadira nati, ‘Pepani, ndakupembani, lezereni mtima, ndidzakubwezerani ndithu zonse.’ Mbuye wake uja adamumveradi chifundo, ndipo adamkhululukira ngongole ija, namlola kuti apite. “Koma pamene wantchitoyo ankatuluka, adakumana ndi mmodzi mwa antchito anzake, yemwe iye adaamkongoza ndalama zochepa. Adamgwira pa khosi mwaukali namuuza kuti, ‘Bweza ngongole yako ija.’ Apo wantchito mnzake uja adadzigwetsa pansi ku mapazi ake nati, ‘Pepani, ndakupembani, lezereni mtima, ndidzakubwezerani.’ Koma iye adakana, nakamponyetsa m'ndende kuti mpaka abweze ndithu ngongoleyo. “Antchito anzake ena ataona zimenezi, adamva chisoni kwambiri. Adapita kukafotokozera mbuye wao zonsezo. Tsono mbuye wakeyo adamuitana namuuza kuti, ‘Wantchito woipa iwe, ine ndinakukhululukira ngongole yonse ija pamene unandidandaulira. Kodi sunayenera kuti iwenso umchitire chifundo wantchito mnzako, monga ndinakuchitira iwe chifundo?’ Motero mbuye wakeyo adapsa mtima kwambiri, nampereka kuti akamzunze mpaka atabweza ngongole yonse ija. “Inunsotu Atate anga akumwamba adzakuchitani zomwezo, aliyense mwa inu akapanda kukhululukira mbale wake ndi mtima wonse.” Yesu atatsiriza kunena mau ameneŵa, adachoka ku Galileya nakafika ku dera la Yudeya kutsidya kwa mtsinje wa Yordani. Anthu ambirimbiri adamtsata, ndipo Iye ankachiritsa odwala kumeneko. Afarisi ena adadza kwa Iye. Tsono kufuna pomupezera chifukwa, adamufunsa kuti, “Kodi nkololedwa kuti munthu asudzule mkazi wake pa chifukwa chilichonse?” Yesu adaŵayankha kuti, “Kodi simunaŵerenge kuti Mulungu amene adalenga anthu pa chiyambi, adalenga wina wamwamuna, wina wamkazi? Ndipo kuti Iye yemweyo adati, ‘Nchifukwa chake mwamuna azisiya atate ake ndi amai ake, nakaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo aŵiriwo adzasanduka thupi limodzi.’ Choncho tsopano salinso aŵiri koma thupi limodzi. Tsono zimene Mulungu wazilumukiza pamodzi, munthu asazilekanitse.” Afarisi aja adamufunsa kuti, “Nanga bwanji Mose adalamula kuti mwamuna azipatsa mkazi wake kalata ya chisudzulo kenaka nkumuchotsa?” Yesu adaŵayankha kuti, “Mose adaakulolani kusudzula akazi anu chifukwa cha kukanika kwanuku. Komatu pa chiyambi sizinali choncho ai. Tsono ndikunenetsa kuti aliyense amene asudzula mkazi wake, osati chifukwa cha chigololo, nakwatira wina, akuchita chigololo.” Ophunzira ake adamuuza kuti, “Ndiyetu ngati zili choncho pakati pa mwamuna ndi mkazi wake, ndi bwino tsono kusakwatira.” Yesu adaŵauza kuti, “Si anthu onse angamvetse zimenezi ai, koma okhawo amene Mulungu aŵathandiza. Paja pali ena amene sangathe kukwatira, chifukwa adabadwa motero. Pali ena amene sangathe kukwatira, chifukwa anthu adaŵafula. Pali enanso amene adachita kusankha okha kusakwatira, kuti azitumikira bwino Mulungu. Yemwe angathe kumvetsa, amvetse.” Anthu ena ankabwera ndi ana kuti Yesu aŵasanjike manja ndi kuŵapempherera, ophunzira ake nkumaŵazazira. Koma Yesu adati, “Alekeni anaŵa azibwera kwa Ine, musaŵaletse. Paja Ufumu wakumwamba ndi wa anthu otere.” Atatero adaŵasanjika manja, kenaka nkumapita. Munthu wina wachinyamata adadza kwa Yesu namufunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi ndizichita chabwino chanji kuti ndikalandire moyo wosatha?” Yesu adamuyankha kuti, “Bwanji ukundifunsa za chimene chili chabwino? Wabwino ndi Mmodzi yekha. Ngati ufuna kukaloŵa ku moyo, uzimvera Malamulo.” Iye adati, “Malamulo ake oti?” Yesu adayankha kuti, “Usaphe, usachite chigololo, usabe, usachite umboni wonama, lemekeza atate ako ndi amai ako, ndiponso konda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.” Munthu uja adati, “Malamulo onseŵa ndakhala ndikuŵatsata, nanga chanditsaliranso nchiyani?” Yesu adamuuza kuti, “Ngati ufuna kukhala wabwino kotheratu, pita, kagulitse zonse zimene uli nazo. Ndalama zake ukapatse anthu osauka, ndipo chuma udzachipeza Kumwamba. Kenaka ubwere, uzidzanditsata.” Koma pamene munthu uja adamva mau ameneŵa, adangochokapo ali wovutika mu mtima, chifukwa anali wolemera kwambiri. Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti nkwapatali kwambiri kuti munthu wolemera adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba. Ndipo ndikunenetsanso kuti nkwapafupi kuti ngamira idzere pa kachiboo ka zingano, kupambana kuti munthu wolemera akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.” Pamene ophunzira aja adamva zimenezi, adadabwa kwambiri nati, “Tsono nanga angathe kupulumuka ndani?” Yesu adaŵayang'ana nati, “Kwa anthu zimenezi nzosatheka, koma zonse nzotheka ndi Mulungu.” Pamenepo Petro adayankhapo kuti, “Ifetu paja tidasiya zonse kuti tizikutsatani. Tsono ndiye kuti tidzalandira chiyani?” Yesu adaŵauza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti Mulungu akadzakonzanso zinthu zonse, Mwana wa Munthu adzakhala pa mpando wake wachifumu ndi waulemerero. Tsono inunso amene mudanditsatanu, mudzakhala pa mipando yachifumu khumi ndi iŵiri mukuweruza mafuko khumi ndi aŵiri a Aisraele. Motero aliyense wosiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amai, kapena ana, kapena minda chifukwa cha Ine, ameneyo adzalandira zonsezo mochuluka kwambiri koposa kale, kenaka adzalandira moyo wosatha. Komatu ambiri amene ali oyambirira adzakhala otsirizira, ndipo amene ali otsirizira adzakhala oyambirira.” “Za Ufumu wakumwamba tingazifanizire motere: Munthu wina adaalaŵirira m'mamaŵa kukalemba anthu okagwira ntchito m'munda wake wamphesa. Adaapangana nawo kuti adzaŵalipira ndalama imodzi yasiliva pa tsiku, naŵatuma kumunda kwake. Pa nthaŵi ya 9 koloko adapitanso, nakapeza ena atangokhala khale pa msika, osagwira ntchito. Adaŵauza kuti, ‘Inunso pitani ku munda wanga wamphesa, ndidzakulipirani moyenerera.’ Iwowo adapitadi. Munthu uja adapitanso pa 12 koloko masana ndi pa 3 koloko, nakachita chimodzimodzi. Pafupi 5 koloko madzulo adapitanso nakapeza enanso akungokhala. Adaŵafunsa kuti, ‘Bwanji mwangokhala khale pano tsiku lonse osagwira ntchito?’ Iwowo adayankha kuti, ‘Chifukwa palibe amene watilemba.’ Iye uja adaŵauza kuti, ‘Inunso pitani ku munda wanga wamphesa.’ “Dzuŵa likuloŵa, mwinimunda uja adauza kapitao wake kuti, ‘Kaŵaitane antchito aja, uŵalipire. Uyambire amene alembedwa potsirizawo, utsirizire oyamba aja.’ Pamene adabwera olembedwa pa 5 koloko yamadzulo aja, aliyense adalandira ndalama imodzi. Tsono pamene olembedwa poyamba aja adabwera, ankaganiza kuti alandira pakulu. Koma nawonso adangolandira aliyense ndalama imodzi. Ndiye iwowo polandira, adayamba kuŵiringula, adati, ‘Aa! Anzathu otsiriziraŵa angogwira ntchito kanthaŵi pang'ono, bwanji mwaŵapatsa malipiro olingana ndi athu, pamene ifeyo tathyoka nayo ntchito tsiku lathunthu, ndi chidzuŵa chonse chija?’ Koma mwinimunda uja adayankha mmodzi mwa iwo kuti, ‘Iwe, inetu sindidakubere ai. Kodi suja tinapangana ndalama yasiliva imodzi? Tenga malipiro ako, uzipita. Mwiniwakene ndafuna kuti ndipatse wolembedwa potsirizayu molingana ndi iwe. Kodi zinthu zanga ndisachite nazo monga ndifunira? Kapenatu ukuipidwa nawo ufulu wanga eti?’ ” Tsono Yesu adati, “Choncho amene ali oyambirira adzakhala otsirizira. Ndipo amene ali otsirizira adzakhala oyambirira.” Pamene Yesu ankapita ku Yerusalemu, adaŵatengera pambali ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja. Pa njira adaŵauza kuti, “Tilitu pa ulendo wopita ku Yerusalemu. Kumeneko Mwana wa Munthu akukaperekedwa kwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo. Iwo akamuweruza ndi kugamula kuti aphedwe, ndipo akampereka kwa anthu akunja. Amenewo akamchita chipongwe, akamkwapula, nkumupachika pa mtanda; koma mkucha wake Iye adzauka kwa akufa.” Pambuyo pake mkazi wa Zebedeo adadza ndi ana ake kwa Yesu, namgwadira kuti ampemphe kanthu. Yesu adamufunsa kuti, “Amai, kodi muli ndi mau?” Iye adayankha kuti, “Ndimati mulonjeze kuti mu Ufumu wanu ana anga aŵiriŵa adzakhale wina ku dzanja lanu lamanja, wina ku dzanja lanu lamanzere.” Koma Yesu adayankha kuti, “Simukudziŵa zimene mukupempha. Kodi inu mungathe kumwa nao chikho chamasautso chimene ndikudzamwera Ine?” Iwo aja adayankha kuti, “Inde, tingathe.” Apo Yesu adati, “Chabwino, mudzamwa nao chikho changacho. Koma Ineyo si udindo wanga kusankha munthu kuti akhale ku dzanja langa lamanja, kapena ku dzanja langa lamanzere. Atate ndiwo adzapereke malo ameneŵa kwa amene Atatewo adaŵakonzera.” Pamene khumi ena aja adamva zimenezi, adapsera mtima abale aŵiri aja. Koma Yesu adaŵaitana ophunzira akewo naŵauza kuti, “Mukudziŵa kuti olamulira amadyera anthu ao masuku pa mutu. Akuluakulu aonso amaonetsadi mphamvu zao pa anthu ao. Koma pakati pa inu zisamatero ai. Aliyense wofuna kukhala mkulu pakati panu, akhale mtumiki wanu. Ndipo aliyense wofuna kukhala mtsogoleri pakati panu, akhale kapolo wanu. Chitani monga m'mene adachitira Mwana wa Munthu: adabwera osati kuti ena adzamtumikire ai, koma kuti Iyeyo adzatumikire anthu ndi kupereka moyo wake kuti aombole anthu ochuluka.” Pamene Yesu ndi ophunzira ake ankatuluka mu mzinda wa Yeriko, anthu ambirimbiri ankamutsatira. Panali anthu aŵiri akhungu amene adaakhala pansi pamphepete pa mseu. Iwo aja atamva kuti Yesu akupita mumseumo, adayamba kufuula kuti, “Inu Ambuye, Mwana wa Davide, mutichitire chifundo.” Anthu aja adaŵazazira akhunguwo kuti akhale chete. Koma iwo nkumafuulirafuulira kuti, “Inu Ambuye, Mwana wa Davide, mutichitire chifundo.” Yesu adaima, naŵaitana, nkuŵafunsa kuti, “Kodi mukufuna kuti ndikuchitireni chiyani?” Iwo aja adati, “Ambuye, tikufuna kuti tizipenya.” Yesu adaŵamvera chifundo nakhudza maso ao. Pompo iwo adayamba kupenya, kenaka nkumamutsata. Pamene iwo ankayandikira ku Yerusalemu, nkufika ku Betefage, ku Phiri la Olivi, Yesu adatuma ophunzira aŵiri, naŵauza kuti, “Pitani m'mudzi mukuwonawo. Mukakangoloŵamo, mukapeza bulu ali chimangire, ndi mwana wake ali naye pamodzi. Mukaŵamasule nkubwera nawo kuno. Wina akakakufunsani kanthu, inu mukati, ‘Ambuye ali nawo ntchito, akangothana nawo aŵatumiza nthaŵi yomweyo.’ ” Zimenezi zidaatero kuti zipherezere zimene mneneri adaanena kuti, “Uzani mzinda wa Ziyoni kuti, ‘Ona mfumu yako ikudza kwa iwe. Ndi yodzichepetsa ndipo yakwera pa bulu. Zoonadi yakwera pa kabulu, mwana wa nyama yosenza katundu.’ ” Tsono ophunzira aja adapitadi nakachita monga momwe Yesu adaaŵalamulira. Adabwera naye bulu ndi mwana wake uja, nayala zovala zao pamsana pa abuluwo, Yesu nkukwerapo. Anthu ambiri ankayala zovala zao mu mseu, ndipo ena adakadula nthambi za mitengo nkumaziyalika mumseumo. Anthu ochuluka amene anali patsogolo, ndi amene anali m'mbuyo, adayamba kufuula kuti, “Ulemu kwa Mwana wa Davide. Ngwodala amene alikudza m'dzina la Ambuye. Ulemu kwa Mulungu kumwambamwamba.” Pamene Yesu adaloŵa mu Yerusalemu, mzinda wonse udatekeseka, ena nkumafunsa kuti, “Kodi ameneyu ndani?” Tsono onse aja adayankha kuti, “Ameneyu ndi mneneri Yesu wochokera ku Nazarete, ku Galileya.” Yesu adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, nayamba kutulutsa onse amene ankachita malonda m'menemo. Adagubudula matebulo a osinthitsa ndalama, ndiponso mipando ya ogulitsa nkhunda. Adaŵauza kuti, “Malembo akuti, ‘Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo.’ Koma inu mukuisandutsa phanga la achifwamba.” Anthu akhungu ndi opunduka adadza kwa Yesu m'Nyumba ya Mulungumo, ndipo Iye adaŵachiritsa. Akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo adaona zodabwitsa zimene Iye ankachita. Adamvanso ana akufuula m'Nyumba ya Mulungu kuti, “Ulemu kwa Mwana wa Davide.” Ndiye iwowo adapsa nazo mtima, nafunsa Yesu kuti, “Kodi mukumva zimene akunenazi?” Yesu adaŵayankha kuti, “Inde. Kani simudaŵerenge konse mau a Mulungu aja akuti, ‘Mudaphunzitsa ana ndi makanda omwe kukutamandani kotheratu?’ ” Pamenepo Yesu adaŵasiya, natuluka mumzindamo kupita ku Betaniya, nakagona kumeneko. M'maŵa mwake, m'mamaŵa ndithu, pamene Yesu ankabwerera ku Yerusalemu, adaamva njala. Ataona mkuyu pambali pa mseu, nkupitapo, sadapezepo chilichonse koma masamba okhaokha. Pamenepo adauza mtengowo kuti, “Mtengo iwe, kuyambira tsopano mpaka muyaya usadzabalenso konse zipatso.” Nthaŵi yomweyo mkuyu uja udachita kuti gwa, kuuma. Pamene ophunzira aja adaona zimenezi, adadabwa nafunsa Yesu kuti, “Mkuyuwu wauma bwanji nthaŵi yomweyi?” Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti ngati mukhala ndi chikhulupiriro, osakayika, mudzachita zimene ndauchita mkuyuzi. Koma si pokhapo ai, ngakhale mutauza phiri ili kuti, ‘Choka apa, kadziponye m'nyanja,’ zidzachitikadi. Ngati mukhala ndi chikhulupiriro, zonse zimene mungapemphe kwa Mulungu mudzalandira.” Yesu adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, ndipo pamene ankaphunzitsa, akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda adadzamufunsa kuti, “Kodi mphamvu zoti muzichita zimenezi mudazitenga kuti? Ndani adakupatsani mphamvu zimenezi?” Yesu adati, “Nanenso ntakufunsani funso limodzi. Mukandiyankha, ndiye ndikuuzeni kumene ndidazitenga mphamvu zoti ndizichita zimenezi. Kodi Yohane kuti azibatiza, mphamvu zake adaazitenga kwa yani, kwa Mulungu kapena kwa anthu?” Iwo aja adayamba kukambirana nkumati, “Tikati adaazitenga kwa Mulungu, Iyeyu anena kuti, ‘Nanga bwanji tsono simudamkhulupirire?’ Komanso tikati adaazitenga kwa anthu, anthuŵa satileka, chifukwatu onse amati Yohane anali mneneri.” Ndiye adangomuyankha Yesuyo kuti, “Kaya, ife sitikudziŵa.” Apo Iye adati, “Nanenso tsono sindikuuzani kumene ndidazitenga mphamvu zoti ndizichita zimenezi.” “Kodi inu, mukuganiza bwanji? Munthu wina anali ndi ana aamuna aŵiri. Adapita kwa woyamba, nakamuuza kuti, ‘Mwana wanga, pita ukagwire ntchito m'munda wamphesa lero.’ Iyeyo adati, ‘Toto ine.’ Koma pambuyo pake adasintha maganizo, napitadi. Bambo uja adapita kwa mwana wina uja, nakamuuza mau omwe aja. Iyeyo adati, ‘Chabwino atate,’ koma sadapite. Kodi mwa aŵiriwo, yemwe adachita zimene bambo wake ankafuna ndi uti?” Iwo adati, “Woyamba uja.” Yesu adaŵauza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti okhometsa msonkho ndi akazi adama akuloŵa mu Ufumu wa Mulungu inu nkumakusiyani m'mbuyo. Paja Yohane Mbatizi adaabwera nadzakuwonetsani njira ya chilungamo, inu osamkhulupirira, m'menemo okhometsa msonkho ndi akazi adama adamkhulupirira. Inuyo ngakhale mudaziwona zimenezo, simudasinthe maganizo pambuyo pake kuti muzimkhulupirira.” Yesu adati, “Imvani fanizo lina. Munthu wina anali ndi munda wake. M'mundamo adaabzalamo mipesa, namanga mpanda kuzinga mundawo. Adakumba nkhuti yoponderamo mphesa, namanga nsanja yolondera mundawo. Pambuyo pake munda uja adaubwereka alimi, iye nkunyamuka ulendo wa ku dziko lina. Nyengo yothyola zipatso itayandikira, munthu uja adatuma antchito ake kwa alimi aja, kuti akatengeko zipatso za m'munda muja. Koma alimiwo adaŵagwira antchito aja, wina kummenya, wina kumupha, wina kumponya miyala. Munthu uja adatumanso antchito ena, ochuluka koposa oyamba aja, ndipo alimi aja adaŵachita chimodzimodzi. Potsiriza pake adaŵatumira mwana wake, nanena kuti, ‘Mwana wanga yekhayu akamchitira ulemu.’ Koma pamene alimiwo adaona mwana wakeyo, adayamba kuuzana kuti, ‘Ameneyu ndiye amene ati adzamsiyire chumachi. Tiyeni timuphe kuti chidzakhale chathu.’ Tsono adamugwiradi, namuponya kunja kwa mundawo, nkumupha. “Kodi mwini munda wamphesa uja akadzafika, adzaŵatani alimi aja?” Iwo adati, “Adzaŵapha moŵazunza alimi oipawo, munda uja nkuubwereka alimi ena amene adzampatsa zipatso zake pa nyengo yake.” Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi monga simudaŵerenge Malembo aja akuti, “ ‘Mwala umene amisiri omanga nyumba adaaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya, wofunika koposa. Ambuye ndiwo adachita zimenezi, ndipo nzotidabwitsa kwambiri.’ “Nchifukwa chake ndikunenetsa kuti Mulungu adzakulandani Ufumu wake ndi kuupereka kwa anthu ena amene adzabala zipatso zoyenera.” [ “Aliyense wogwera pa mwala umenewu, adzasanduka zidutswa zokhazokha. Ndipo aliyense amene mwalawu udzamugwere, udzangomutswanyiratu.”] Pamene akulu a ansembe ndi Afarisi adamva mafanizo ameneŵa a Yesu, adazindikira kuti ankanena iwowo, motero adafuna kumugwira. Koma ankaopa anthu, popeza kuti ochuluka ankakhulupirira kuti Yesu ndi mneneri. Yesu adalankhulanso ndi anthu aja m'mafanizo. Adati, “Za Ufumu wakumwamba tingazifanizire motere: Mfumu ina idaakonzera mwana wake phwando laukwati. Idatuma antchito ake kuti akaŵauze anthu amene adaaitanidwa kuphwandoko kuti azibwera, anthuwo nkukana. Idatumanso antchito ena nkunena kuti, ‘Kaŵauzeni oitanidwa aja kuti chakudya chakonzeka. Ndapha ng'ombe ndi nyama zina zonenepa. Zonse zakonzeka, bwerani ku phwando laukwati.’ Koma oitanidwawo sadalabadireko, adangopita ku zao: wina kumunda kwake, wina ku ntchito yake yamalonda. Enawo adagwira antchito a mfumu aja naŵazunza, nkuŵapha. “Pamenepo mfumu idapsa mtima kwambiri, mwakuti idatuma ankhondo ake kuti akaononge opha anzao aja, ndi kutentha mudzi wao. Pambuyo pake idauza antchito ake kuti, ‘Phwando laukwati ndiye lakonzekatu, koma oitanidwa aja anali osayenera. Pitani tsono ku mphambano za miseu, mukaitane aliyense amene mukampeze, kuti abwere kuno ku phwando laukwati.’ Apo antchitowo adapitadi ku miseu nakasonkhanitsa onse amene adaŵapeza, abwino ndi oipa omwe, mwakuti nyumba yaphwando idadzaza ndi anthu. “Pamene mfumu ija idaloŵa m'nyumbamo kukaona anthu odzadya phwando aja, idapezamo wina amene sadavale chovala chaukwati. Tsono idamufunsa kuti ‘Kodi iwe, waloŵa bwanji muno opanda chovala chaukwati?’ Iye uja adangoti chete. Apo mfumuyo idauza anyamata ake kuti, ‘Mmangeni manja ndi miyendo, mukamponye kunja ku mdima. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.’ ” Tsono Yesu adati, “Inde oitanidwa ngambiri, komatu osankhidwa ngoŵerengeka.” Nthaŵi ina Afarisi adakapangana zodzatapa Yesu m'kamwa. Adatuma ophunzira ao ena pamodzi ndi ena a m'chipani cha Herode kwa Yesu. Iwoŵa adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, tikudziŵa kuti Inu mumanena zoona, mumaphunzitsa malamulo a Mulungu moona, ndipo simuwopa munthu aliyense. Paja Inu simuyang'anira kuti uyu ndani. Ndiye timati mutiwuze zimene mukuganiza. Kodi Malamulo a Mulungu amatilola kuti tizikhoma msonkho kwa Mfumu ya ku Roma, kapena ai?” Koma Yesu podziŵa maganizo ao oipa, adati, “Bwanji kodi mukundiyesa dala, anthu achiphamasonu? Tandiwonetsani ndalama yamsonkho.” Iwo adampatsadi ndalamayo. Pamenepo Iye adaŵafunsa kuti, “Kodi nkhopeyi ndi ya yani, ndipo dzinali ndi la yani?” Iwo aja adati, “Zonse ndi za Mfumu ya ku Roma.” Apo Yesu adaŵauza kuti, “Tsono perekani kwa Mfumu zake za Mfumuyo, ndiponso kwa Mulungu zake za Mulungu.” Atamva zimenezi, anthuwo adathedwa nzeru, motero adamsiya nachokapo. Tsiku lomwelo Asaduki ena adadza kwa Yesu. (Paja iwo amati akufa sadzauka.) Adamufunsa kuti, “Aphunzitsi, Mose adati, ‘Ngati munthu amwalira opanda ana, mbale wake wa womwalirayo aloŵe chokolo, kuti amuberekere ana mbale wake uja.’ Tsono kwathu kudaali anthu asanu ndi aŵiri pachibale pao. Woyamba adaakwatira mkazi, nkumwalira. Tsono popeza kuti analibe mwana, adasiyira mbale wake mkazi wake uja. Chimodzimodzinso wachiŵiri ndi wachitatu, mpaka wachisanu ndi chiŵiri. Potsiriza pake mai uja nayenso adamwalira. Nanga tsono pa tsiku lodzauka akufa, mwini mkaziyo adzakhala utiwuti pakati pa abale asanu ndi aŵiri aja, popeza kuti onsewo adaamkwatirapo?” Yesu adaŵayankha kuti, “Mukulakwa chifukwa simudziŵa Malembo, ngakhalenso mphamvu za Mulungu. Pajatu pouka akufa, palibenso za kukwatira kapena kukwatiwa ai. Onse ali ngati angelo Kumwamba. Tsono zakuti anthu adzauka kwa akufa, kodi simudaŵerenge zimene Mulungu adakuuzani zija kuti, ‘Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, ndine Mulungu wa Isaki, ndine Mulungu wa Yakobe?’ Ndiye kutitu sali Mulungu wa anthu akufa ai, koma wa anthu amoyo.” Pamene anthu ochuluka aja amene anali pamenepo adamva zimenezi, adadabwa kwambiri ndi zophunzitsa zake. Afarisi atamva kuti Yesu adatsutsa Asaduki, adasonkhana. Tsono mmodzi mwa iwo, katswiri wa Malamulo, adafunsa Yesu funso kuti amutape m'kamwa. Adati, “Aphunzitsi, kodi mwa malamulo onse a Mulungu, lalikulu ndi liti?” Yesu adamuyankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. Limeneli ndiye lamulo lalikulu ndi loyamba ndithu. Lachiŵiri lake lofanana nalo ndi ili: Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe. Malamulo onse a Mose ndiponso zonse zimene aneneri adaphunzitsa zagona pa malamulo aŵiriŵa.” Afarisi atasonkhana pamodzi, Yesu adaŵafunsa funso. Adati, “Mumaganiza chiyani za Mpulumutsi wolonjezedwa uja? Mumati ndi mwana wa yani?” Iwo aja adati, “Ndi mwana wa Davide.” Iye adaŵafunsa kuti, “Tsono bwanji nanga Davideyo ndi nzeru zochokera kwa Mzimu Woyera, akutchula Mpulumutsi wolonjezedwa uja kuti Mbuye wake? Paja adati, “ ‘Chauta adauza Mbuye wanga kuti, Khala ku dzanja langa lamanja, mpaka nditasandutsa adani ako kuti akhale ngati chopondapo mapazi ako.’ “Ngati Davide akutchula Mpulumutsi wolonjezedwa uja kuti Mbuye wake, angakhale mwana wakenso bwanji?” Panalibe ndi mmodzi yemwe wotha kumuyankha ngakhale mau amodzi. Tsono kuyambira tsiku limenelo panalibenso munthu amene adalimba mtima kuti amufunse mafunso. Pambuyo pake Yesu adalankhula ndi gulu la anthu ochuluka pamodzi ndi ophunzira ake. Adaŵauza kuti, “Aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi ali ndi udindo wotanthauzira malamulo a Mose. Nchifukwa chake muzichita ndi kutsata zonse zimene iwo amakuphunzitsani. Komatu musamatsanzira zimene amachita, pakuti sachita zimene amaphunzitsa. Iwo amamanga katundu wosautsa kunyamula nkusenzetsa anthu, koma iwowo samukhudzako mpang'ono pomwe. Zonse zimene amachita amangozichita kuti anthu aŵaone. Amadzimangirira timapukusi tikulutikulu ta mau a Mulungu pa mphumi ndi pa mkono. Amatalikitsanso mphonje za zovala zao. Amakonda malo olemekezeka pa maphwando ndiponso mipando yaulemu kwambiri ku nyumba zamapemphero. Amakondanso kuti anthu aziŵalonjera mwaulemu pa misika, ndipo kuti aziŵatchula aphunzitsi. “Koma inuyo anthu asati azikutchulani aphunzitsi, pakuti muli ndi Mphunzitsi mmodzi yekha, ndipo nonsenu muli pa chibale. Musamatchulanso munthu pansi pano kuti atate, popeza kuti muli ndi atate amodzi okha, ndiwo Atate anu akumwamba. Anthu asatinso azikutchulani atsogoleri, popeza kuti Mtsogoleri wanu ndi mmodzi yekha, ndiye Khristu. Pakati panupa wamkulu akhale mtumiki wanu. Pajatu aliyense wodzikuza adzamchepetsa, ndipo aliyense wodzichepetsa adzamkuza.” “Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumatseka pakhomo pa Ufumu wakumwamba kuti anthu asaloŵemo. Paja inu nomwe simuloŵamo, ndipo mumatsekereza amene amafuna kuloŵamo.” [ “Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumagongolera azimai amasiye nkumaŵadyera chuma chao, kwinaku nkumanyengezera kunena mapemphero ataliatali. Chifukwa cha zimenezi Mulungu adzakulangani koposa.”] “Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumayenda maulendo ambirimbiri pa nyanja ndi pa mtunda, kufunafuna ngakhale munthu mmodzi yekha kuti atembenuke ndi kusanduka wophunzira wanu. Tsono akapezeka, mumamsandutsa woyenera kulangidwa ku Gehena kuposa inu kaŵiri. “Muli ndi tsoka, inu atsogoleri akhungu! Inu mumati, ‘Munthu akalumbira kuti, Pali Nyumba ya Mulungu, lumbirolo nlachabe. Koma akalumbira kuti, Pali chuma cha m'Nyumba ya Mulungu, asunge lumbiro lakelo.’ Inu anthu opusa ndi akhungu! Chachikulu nchiti, chuma chija, kapena Nyumba imene ikusandutsa chumacho kuti chikhale chopatulika? Mumatinso, ‘Munthu akalumbira kuti, Pali guwa lansembe, lumbirolo nlachabe. Koma akalumbira kuti, Pali choperekedwa pa guwa, asunge lumbiro lakelo.’ Anthu akhungu inu! Chachikulu nchiti, choperekedwa chija, kapena guwa lansembe lija limene likusandutsa choperekedwacho kuti chikhale chopatulika? Tsonotu munthu akalumbira kuti, Pali guwa la nsembe, walumbiranso pa zonse zimene zili paguwapo. Akalumbira kuti, Pali Nyumba ya Mulungu, walumbiranso pa zonse zimene zili m'Nyumbamo. Ndipo akalumbira kuti, Kumwambadi, walumbiranso pa mpando wachifumu wa Mulungu, ndiponso pa Iye amene amakhala pampandopo. “Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumapereka chachikhumi cha timbeu tonunkhira, ndi cha timbeu tokometsera chakudya, koma simusamala zazikulu zenizeni pa Malamulo a Mulungu, monga kuweruza molungama, kuchita zachifundo, ndi kukhala okhulupirika. Mukadayenera kuchitadi zimenezi, komabe osasiya zinazo. Inu atsogoleri akhungu, mumasuza zakumwa zanu kuti muchotsemo kanchenche, koma mumameza ngamira. “Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumatsuka kunja kwa chikho ndi kwa mbale koma m'kati mwake m'modzaza ndi nzeru zakuba, ndi zaumbombo. Afarisi akhungu inu, yambani mwatsuka m'kati mwa chikho, ndipo kunja kwakenso kudzayera. “Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Muli ngati manda opaka njeresa, amene amaoneka okongola kunja, pamene m'kati mwake m'modzaza ndi mafupa a anthu akufa ndi zoola zina zilizonse. Inunso muli chimodzimodzi: pamaso pa anthu mumaoneka olungama, pamene m'kati mwanu m'modzaza ndi chiphamaso ndi zoipa zina. “Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumakonza bwino manda a aneneri, ndipo mumakongoletsa ziliza za anthu olungama. Ndiye mumati, ‘Tikadakhala ndi moyo pa nthaŵi ya makolo athu ija, sibwenzi ife titaŵapha nao aneneriwo ai.’ Koma potero mukuvomera nokha kuti ndinu zidzukulu za anthu amene adapha aneneriwo. Chabwino tsono, itsirizeni ntchitoyo imene makolo anu aja adaiyamba.” “Njoka inu, ana a mamba, mudzachipeŵa bwanji chilango cha ku Gehena? Mvetsetsani tsono! Ine ndidzakutumizirani aneneri, ndiponso anthu anzeru ndi aphunzitsi. Ena mudzaŵapha ndi kuŵapachika pa mtanda. Ena mudzaŵakwapula m'nyumba zanu za mapemphero, ndipo mudzaŵazunza pakuŵapirikitsa kuchokera ku mudzi wina mpaka ku mudzi wina. Motero chilango chidzakugwerani chifukwa cha anthu olungama onse amene adaphedwa, kuyambira kuphedwa kwa Abele, munthu wolungama uja, mpaka kuphedwa kwa Zakariya, mwana wa Barakiya, amene mudamuphera m'Nyumba ya Mulungu pakati pa guwa lansembe ndi Malo Opatulika kopambana. Ndithu ndikunenetsa kuti chilango cha zonsezi chidzaŵagwera ndithu anthu amakonoŵa.” “Iwe Yerusalemu, Yerusalemu! Umapha aneneri, nkuŵaponya miyala anthu amene Mulungu amakutumizira. Nkangati ndakhala ndikufuna kusonkhanitsa anthu ako, monga momwe nkhuku imasonkhanitsira anapiye ake pansi pa mapiko ake, iwe nkumakana! Ndithu nyumba yanu yaikuluyi idzasanduka bwinja. Ndipo ndikunenetsa kuti simudzandiwonanso konse mpaka mudzati, ‘Ngwodala amene alikudza m'dzina la Ambuye.’ ” Yesu adatuluka m'Nyumba ya Mulungu, ndipo pamene ankachoka, ophunzira ake adabwera nkumamuwonetsa kamangidwe ka Nyumbayo. Koma Yesu adaŵauza kuti, “Nanga simukuziwona zonsezi? Ndithu ndikunenetsa kuti sipadzatsala konse mwala ndi umodzi womwe pamwamba pa mwala unzake: yonse adzaigumula.” Tsono Yesu atakhala pansi, pa Phiri la Olivi, ophunzira ake adadza kwa Iye paokha. Adamufunsa kuti, “Tatiwuzani, zimenezi zidzachitika liti? Tidzaonera chiyani kuti nthaŵi yakwana ya kubweranso kwanu, ndiponso ya kutha kwa dziko lapansi?” Yesu adaŵayankha kuti, “Chenjerani kuti wina aliyense asadzakusokezeni. Chifukwa kudzafika anthu ambiri m'dzina langa namadzanena kuti, ‘Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndine,’ ndipo adzasokeza anthu ambiri. Mudzamva phokoso la nkhondo za kufupi kuno ndi mphekesera za nkhondo zakutali. Ndiye inu musadzade nkhaŵa. Zimenezi zidzayenera kuchitika, koma sindiye kuti chimalizo chija chafika kale ai. Mitundu yosiyanasiyana idzaukirana, maiko osiyanasiyana adzamenyana nkhondo. Kudzakhala njala, ndipo kudzachita zivomezi ku malo osiyanasiyana. Tsono zonsezitu nkuyamba chabe kwa mavuto. “Pambuyo pake anthu adzakuperekani kuti mukazunzidwe, kenaka adzakuphani. Anthu a mitundu yonse ya anthu adzadana nanu chifukwa cha Ine. Pa nthaŵi imeneyo ambiri adzataya chikhulupiriro chao, azidzaperekana nkumadana. Kudzaoneka aneneri onama ambiri, amene azidzasokeza anthu ambiri. Tsono popeza kuti zoipa zizidzachulukirachulukira, chikondi chizidzacheperachepera pakati pa anthu. Koma yemwe adzalimbikire mpaka potsiriza, ameneyo ndiye adzapulumuke. Ndipo Uthenga Wabwinowu wonena za ufumu wa Mulungu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi, kuti anthu a mitundu yonse apezepo umboni. Pamenepo ndiye chimalizo chidzafike.” “Mudzaona ‘Chosakaza chonyansa chija’ chimene mneneri Daniele adaanena, atachiimika m'Nyumba ya Mulungu. (Amene ukuŵerengawe, umvetse bwino.) Pamenepo amene ali ku Yudeya athaŵire ku mapiri. Amene ali padenga pa nyumba yake, asatsike nkuloŵanso m'nyumba mwake kuti akatenge katundu. Yemwe ali ku munda, asabwererenso ku nyumba kuti akatenge mwinjiro. Ali ndi tsoka azimai amene adzakhale ndi pathupi, ndiponso azimai oyamwitsa ana masiku amenewo. Pempherani kuti nthaŵi pamene muzidzathaŵa, isadzakhale nyengo yachisanu, kapena pa tsiku la Sabata. Chifukwa masautso amene adzaoneka masiku amenewo, sanaonekepo chilengedwere dziko lapansi mpaka pano, ndipo sadzaonekanso. Masiku amenewo, akadapanda kuŵachepetsa, sakadapulumukapo munthu ndi mmodzi yemwe. Koma Mulungu adzaŵachepetsa masikuwo chifukwa cha anthu amene Iye adaŵasankha. “Pa nthaŵi imeneyo wina akadzakuuzani kuti, ‘Ali panotu Khristu uja! Uyo ali apoyo!’ musadzakhulupirire. Chifukwa kudzaoneka anthu onama omanena kuti ‘Ndine Khristu uja,’ kapena kuti, ‘Ndine mneneri.’ Anthuwo azidzachita ntchito zamphamvu ndiponso zinthu zozizwitsa, kuti ngati nkotheka asokeze ngakhale osankhidwa a Mulungu. Mvetsetsani, Ine ndiye ndakuuziranitu zimenezi. “Nchifukwa chake, anthu akadzakuuzani kuti, ‘Inu, Khristu ali ku chipululu,’ musadzapiteko. Kapena akadzati, ‘Ali m'kati mwa nyumba,’ musadzakhulupirire. Mwana wa Munthutu kubwera kwake kudzakhala monga muja mphezi imang'animira ndi kuŵala kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe. “Paja adati, Kulikonse kumene kwafera chinthu, miphamba imasonkhana kumeneko.” “Akadzangotha mavuto a masiku amenewo, dzuŵa lidzada, mwezi udzaleka kuŵala, nyenyezi zidzagwa kuchokera ku thambo, ndipo mphamvu zamumlengalenga zidzagwedezeka. Pamenepo chizindikiro cha Mwana wa Munthu chidzaoneka ku thambo. Anthu a mitundu yonse ya pansi pano adzayamba kulira, ndipo adzaona Mwana wa Munthu akubwera pa mitambo ali ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu. Kudzamveka lipenga lamphamvu, ndipo Iye adzatuma angelo ake, kuti akasonkhanitse osankhidwa ake kuchokera ku mbali zonse, kuyambira ku malekezero ena a dziko lapansi mpaka ku malekezero ake enanso.” “Yang'anani mkuyu kuti mutengerepo phunziro. Mukamaona kuti nthambi zake zayamba kukhala zanthete, ndipo masamba akuphuka, mumadziŵa kuti chilimwe chayandikira. Momwemonso, mukadzaona zonse ndanena zija, mudzadziŵe kuti Mwana wa Munthu ali pafupi, ali pakhomo penipeni. Ndithu ndikunenetsa kuti zonsezi zidzaoneka anthu a mbadwo unoŵa asanamwalire onse. Thambo ndi dziko lapansi zidzatha, koma mau anga sadzatha mphamvu konse.” “Koma za tsiku lake kapena nthaŵi yake, palibe amene amadziŵa. Angelo omwe akumwamba sadziŵa. Ngakhale Ineyo Mwanane sindidziŵa; amadziŵa ndi Atate okha basi. Kudza kwa Mwana wa Munthu kudzakhala monga momwe zinthu zidaayendera pa nthaŵi ya Nowa. Masiku amenewo, chisanafike chigumula, anthu ankangodya ndi kumwa, ankakwatira ndi kukwatiwa, mpaka tsiku limene Nowa adaloŵa m'chombo. Sadazindikire kanthu mpaka chigumula chidafika nkuŵaononga onse. Zidzateronso pamene Mwana wa Munthu adzabwera. Pa nthaŵi imeneyo anthu aŵiri adzakhala ali m'munda, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya. Azimai aŵiri adzakhala akusinja, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya. “Nanunso tsono, khalani maso, chifukwa simudziŵa tsiku limene Ambuye anu adzabwere. Koma dziŵani kuti mwini nyumba akadadziŵa nthaŵi yofika mbala, bwenzi atakhala maso, osalola kuti mbala imuthyolere nyumba. Choncho inunso muzikhala okonzeka, pakuti Mwana wa Munthu adzabwera pa nthaŵi imene inu simukuyembekeza.” “Tsono wantchito wokhulupirika ndi wanzeru ndani, amene mbuye wake adamuika kuti aziyang'anira onse a m'nyumba mwake, nkumaŵagaŵira chakudya chao pa nthaŵi yake? Ngwodala wantchito ameneyo, ngati mbuye wake pofika adzampeza akuchitadi zimenezi. Ndithu ndikunenetsa kuti adzamuika woyang'anira chuma chake chonse. Koma ngati ndi wantchito woipa, mumtima mwake azidzati, ‘Mbuye wanga akuchedwa.’ Ndiye adzayamba kumenya antchito anzake, ndiponso kumadya ndi kumamwa pamodzi ndi zidakwa. Tsono mbuye wake adzangoti mbwe mwadzidzidzi, pa tsiku limene iye sakumuyembekeza. Choncho adzamlanga koopsa, ndipo adzamtaya ku malo a anthu achiphamaso. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.” “Pa nthaŵi imeneyo za Ufumu wakumwamba zidzafanafana ndi zimene zidaachitikira anamwali khumi. Iwowo adaatenga nyale zao nkumakachingamira mkwati. Asanu anali opusa, ndipo asanu enawo anali ochenjera. Asanu opusa aja adangotenga nyale zao, osatenga mafuta ena apadera. Koma asanu ochenjera aja adaatenga mafuta ena apadera m'nsupa zao. Popeza kuti mkwati adaachedwa, onse aja adayamba kuwodzera, nagona tulo. “Tsono pakati pa usiku kudamveka kufuula kuti, ‘Mkwati akubwera! Tulukani, kamchingamireni!’ Anamwali khumi aja adadzuka, nkuyamba kukonza nyale zao zija. Opusa aja adapempha ochenjera aja kuti, ‘Tipatseniko mafuta, onani nyale zathu zikuzima.’ Koma ochenjera aja adati, ‘Hi, ai, tikatero satikwanira tonsefe. Bwanji osati mungopita ku sitoro mukagule anu.’ Pamene ankakagula, mkwati adafika. Amene anali okonzekeratu aja adaloŵa naye pamodzi m'nyumba yaphwando; pambuyo pake adatseka chitseko. “Kenaka m'mbuyomwalendo anamwali ena aja nawonso adabwera nati, ‘Bwana, Bwana, titsekulireni!’ Koma mkwatiyo adati, ‘Pepani, sindikukudziŵani!’ ” Pomaliza Yesu adati, “Ndiyetu inu, muzikhala maso, poti simudziŵa tsiku lake kapena nthaŵi yake.” “Za Ufumu wakumwamba tingazifanizirenso motere: Munthu wina ankapita pa ulendo. Asananyamuke adaitana antchito ake, naŵasiyira chuma chake. Wina adampatsa ndalama zisanu, wina ziŵiri, wina imodzi. Aliyense adampatsa molingana ndi nzeru zake, iye nkuchokapo. Wantchito amene adaalandira ndalama zisanu uja adapita nakachita nazo malonda nkupindula ndalama zinanso zisanu. Chimodzimodzinso amene adaalandira ndalama ziŵiri uja, adapindula ndalama zinanso ziŵiri. Koma amene adaalandira ndalama imodzi uja, adapita nakaikumbira pansi ndalama ya mbuye wake ija. “Patapita nthaŵi yaitali, mbuye wao uja adabwerako naŵaitana antchito ake aja kuti amufotokozere za zimene adaachita ndi ndalama zija. Wantchito amene adaalandira ndalama zisanu uja adabwera ndi zisanu zinanso nati, ‘Ambuye, mudaandisiyira ndalama zisanu. Onani, ndidapindula zisanu zinanso: izi.’ Mbuye wakeyo adamuuza kuti, ‘Udachita bwino kwabasi, ndiwe mtumiki wabwino ndi wokhulupirika. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika kuti uziyang'anira zinthu zambiri. Bwera udzakondwere pamodzi ndi ine, mbuye wako.’ Nayenso wantchito amene adaalandira ndalama ziŵiri uja, adabwera nati, ‘Ambuye, mudaandisiyira ndalama ziŵiri. Onani, ndidapindula ziŵiri zinanso: izi.’ Mbuye wakeyo adamuuza kuti, ‘Udachita bwino, ndiwe mtumiki wabwino ndi wokhulupirika. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika kuti uziyang'anira zinthu zambiri. Bwera udzakondwere pamodzi ndi ine, mbuye wako.’ “Nayenso amene adaalandira ndalama imodzi uja adabwera nati, ‘Ambuye, ine ndinkadziŵa kuti inu ndinu munthu wankhwidzi. Mumakolola kumene simudabzale, ndipo mumasonkhanitsa dzinthu kumene simudafese mbeu. Ndiye ndinkachita mantha, choncho ndidaakaikumbira pansi ndalama yanu ija. Nayi tsono ndalama yanuyo.’ Apo mbuye wake uja adamuuza kuti, ‘Ndiwe wantchito woipa ndi waulesi. Kani unkadziŵa kuti ineyo ndimakolola kumene sindidabzale, ndipo ndimasonkhanitsa dzinthu kumene sindidafese mbeu? Tsonotu udaayenera kukaiika ku banki ndalama yangayo, ine pobwera ndikadadzailandira pamodzi ndi chiwongoladzanja chake. Mlandeni ndalamayi, muipereke kwa amene ali ndi ndalama khumiyo. Pajatu aliyense amene ali ndi kanthu, adzamuwonjezera zina, choncho adzakhala ndi zochuluka koposa. Koma amene alibe kanthu, ngakhale kamene ali nakoko adzamlandabe. Tsono mtumiki wopandapakeyu kamponyeni kunja ku mdima. Kumeneko azikalira ndi kukukuta mano.’ “Pamene Mwana wa Munthu adzabwera ndi ulemerero wake, pamodzi ndi angelo onse, adzachita kukhalira pa mpando wake wachifumu. Adzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse pamaso pake, ndipo adzaŵalekanitsa monga momwe mbusa amalekanitsira nkhosa ndi mbuzi. Nkhosa adzazikhazika ku dzanja lake lamanja, koma mbuzi ku dzanja lake lamanzere. Tsono Iyeyo ngati Mfumu adzauza a ku dzanja lamanjawo kuti, ‘Bwerani kuno inu odalitsidwa a Atate anga. Loŵani mu ufumu umene adakukonzerani chilengedwere dziko lapansi. Paja Ine ndidaali ndi njala, inu nkundipatsa chakudya. Ndidaali ndi ludzu, inu nkundipatsa chakumwa. Ndidaali mlendo, inu nkundilandira kunyumba kwanu. Ndidaali wamaliseche, inu nkundiveka. Ndinkadwala, inu nkumadzandizonda. Ndidaali m'ndende, inu nkumadzandichezetsa.’ Apo olungama aja adzati, ‘Ambuye, ndi liti tidaakuwonani muli ndi njala, ife nkukupatsani chakudya, kapena muli ndi ludzu, ife nkukupatsani chakumwa? Ndi liti tidaakuwonani muli mlendo, ife nkukulandirani kunyumba kwathu, kapena muli wamaliseche, ife nkukuvekani? Ndi liti tidaamvapo kuti mukudwala kapena kuti muli m'ndende, ife nkudzakuchezetsani?’ Mfumuyo idzaŵayankha kuti, ‘Ndithu ndikunenetsa kuti nthaŵi iliyonse pamene munkamuchitira zimenezi wina aliyense mwa abale anga ngakhale otsika kwambiriŵa, munkachitira Ine amene.’ “Pambuyo pake Mfumuyo idzauzanso a ku dzanja lake lamanzere aja kuti, ‘Chokani apa, inu otembereredwa. Pitani ku moto wosatha, umene Mulungu adakonzera Satana ndi angelo ake. Ine ndidaali ndi njala, inu osandipatsa chakudya. Ndidaali ndi ludzu, inu osandipatsa chakumwa. Ndidaali mlendo, inu osandilandira kunyumba kwanu. Ndidaali wamaliseche, inu osandiveka. Ndinkadwala, ndidaalinso m'ndende, inu osadzandichetsa.’ Apo nawonso adzati, ‘Ambuye, ndi liti tidaakuwonani muli ndi njala, kapena muli ndi ludzu, kapena wamaliseche, ndi liti tidaamvapo kuti mukudwala kapena kuti muli m'ndende, ife osachitapo kanthu?’ Mfumuyo idzaŵayankha kuti, ‘Ndithu ndikunenetsa kuti, nthaŵi iliyonse pamene munkakana kuthandiza wina aliyense mwa abale anga ngakhale otsika kwambiriŵa, munkakana kuthandiza Ine amene.’ Pamenepo iwowo adzachoka kumapita ku chilango chosatha, olungama aja nkumapita ku moyo wosatha.” Yesu atatsiriza kulankhula nkhani zonsezi, adauza ophunzira ake kuti, “Pajatu chikondwerero cha Paska chiyambika patangopita masiku aŵiri, ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kuti akapachikidwe pa mtanda.” Nthaŵi imeneyo akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda adasonkhana m'nyumba ya mkulu wa ansembe onse, dzina lake Kayafa. Ankakambirana za njira yoti agwirire Yesu mochenjera, nkumupha. Koma ankati, “Zimenezi tisadzachite pa nthaŵi ya chikondwerero ai, pangadzachitike chipolowe pakati pa anthu.” Tsiku lina Yesu anali ku Betaniya, m'nyumba ya Simoni wotchedwa Wakhate. Pamene ankadya, kudafika mai wina atatenga nsupa yagalasi ya mafuta onunkhira amtengowapatali. Adayamba kuthira mafutawo pamutu pa Yesu. Koma pamene ophunzira ake adaona zimenezi, adaipidwa nazo nkumauzana kuti, “Chifukwa chiyani kusakaza zinthu chotere? Ndithu mafuta ameneŵa akadatha kuŵagulitsa pa mtengo waukulu zedi, kenaka ndalama zake nkukapatsa anthu osauka.” Yesu podziŵa zimene iwo aja ankalankhula, adaŵafunsa kuti, “Mukumuvutiranji maiyu? Zimenetu wandichitira iyeyuzi nzabwino kwambiri. Anthu osauka muli nawo nthaŵi zonse, koma Ine simudzakhala nane nthaŵi zonse. Iyeyu wathira mafuta ameneŵa pa thupi langa kuti alidzozeretu lisanaikidwe m'manda. Ndithu ndikunenetsa kuti kulikonse kumene anthu azikalalika Uthenga Wabwinowu pa dziko lonse lapansi, azikafotokozanso zimene maiyu wachita, kuti anthu azidzamkumbukira.” Pambuyo pake Yudasi Iskariote, mmodzi mwa ophunzira khumi ndi aŵiri aja, adapita kwa akulu a ansembe. Adakaŵafunsa kuti, “Kodi mudzandipatsa chiyani ndikadzampereka Yesuyu kwa inu?” Iwo adamupatsa ndalama zasiliva makumi atatu. Tsono kuyambira pomwepo iye adayamba kufunafuna mpata womuperekera kwa iwo. Pa tsiku loyamba la masiku a buledi wosafufumitsa, ophunzira aja adadza nafunsa Yesu kuti, “Kodi tikakukonzereni kuti malo okadyerako phwando la Paska?” Iye adaŵauza kuti, “Pitani m'mudzimu kwa munthu wina wake. Mukanene kuti, ‘Aphunzitsi akuti nthaŵi yao ili pafupi, akudzadyera kwanu kuno phwando la Paska pamodzi ndi ophunzira ao.’ ” Ophunzira aja adapita nakachita zomwe Yesu adaaŵauza, nakakonzadi za phwando la Paska. Kutada, Yesu ndi ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja adakhala pamodzi nkumadya. Iwowo alikudya, Yesu adaŵauza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti wina mwa inu andipereka kwa adani anga.” Ophunzirawo adamva chisoni kwambiri, nayamba mmodzimmodzi kumufunsa kuti, “Monga nkukhala ine, Ambuye?” Yesu adaŵayankha kuti, “Yemwe wasunsa mkate m'mbalemu pamodzi ndi Ine, ameneyo ndiye andipereke. Mwana wa Munthu akukaphedwadi, monga momwe Malembo akunenera za Iye. Komabe ali ndi tsoka munthu amene akukapereka Mwana wa Munthuyo. Kukadakhala bwino koposa kwa munthu ameneyo, akadapanda kubadwa.” Yudasi, amene pambuyo pake adapereka Yesu, adafunsa kuti, “Monga nkukhala ine, Aphunzitsi?” Yesu adamuyankha kuti, “Wanena wekha.” Iwo alikudya choncho, Yesu adatenga mkate, nathokoza Mulungu, nkuunyemanyema, nagaŵira ophunzira aja, ndipo adati, “Kwayani, idyani, ili ndi thupi langa.” Kenaka adatenga chikho, nathokoza Mulungu nkuchipereka kwa ophunzirawo. Adaŵauza kuti, “Imwani nonsenu. Pakuti aŵa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi ameneŵa ndiŵakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao. Kunena zoona, kuyambira tsopano sindidzamwanso chakumwa cha mtengo wamphesachi, mpaka tsiku limene ndidzamwe chatsopano pamodzi nanu mu Ufumu wa Atate anga.” Tsono ataimba nyimbo yotamanda Mulungu, onse adatuluka nkumapita ku Phiri la Olivi. Pambuyo pake Yesu adaŵauza kuti, “Nonsenu mukhumudwa nane nkundisiya usiku uno. Paja Malembo akuti, ‘Ndidzapha mbusa, ndipo nkhosa za msambiwo zidzangoti balala.’ Koma ndikadzauka kwa akufa, ndidzatsogola ndine kupita ku Galileya.” Petro adati, “Ngakhale onse akhumudwe nkukusiyani, ine ndekha ai.” Yesu adamuuza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti usiku womwe uno, tambala asanalire, ukhala utandikana katatu kuti Ine sundidziŵa.” Koma Petro adamuuza kuti, “Ngakhale atati andiphere nanu kumodzi, ine sindingakukaneni konse kuti sindikudziŵani.” Ophunzira ena onse aja nawonso adanena chimodzimodzi. Yesu adapita ndi ophunzira ake aja ku malo ena otchedwa Getsemani. Tsono adauza ophunzirawo kuti, “Inu bakhalani pano, Ine ndikupita uko kukapemphera.” Adatengako Petro ndi ana aŵiri aja a Zebedeo. Yesu adayamba kugwidwa ndi chisoni ndi kuvutika mu mtima. Adaŵauza kuti, “Mumtima mwanga muli chisoni chachikulu chofa nacho. Inu khalani pompano, komatu mukhale maso pamodzi nane.” Adapita patsogolo pang'ono, nadzigwetsa choŵeramitsa nkhope pansi nkuyamba kupemphera. Adati, “Atate, ngati nkotheka, chindichokere chikho chamasautsochi. Komabe chitani zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.” Atatero adabwerera kwa ophunzira aja, naŵapeza ali m'tulo. Tsono adafunsa Petro kuti, “Mongadi nonsenu mwalephera kukhala maso pamodzi nane ngakhale pa kanthaŵi kochepa? Khalani maso inu ndi kumapemphera, kuti mungagwe m'zokuyesani. Mtima ndiye ukufunitsitsadi, koma langokhala lofooka ndi thupi.” Adachokanso kachiŵiri nakapemphera kuti, “Atate, ngati chikho chamasautsochi sichingandichoke, mpaka nditamwa ndithu, chabwino, zimene mukufuna zichitike.” Pamene adabwerakonso, adaŵapeza ali m'tulo, chifukwa zikope zao zinkalemera. Yesu adaŵasiyanso, napita kukapemphera kachitatu, akunena mau amodzimodzi omwe aja. Pambuyo pake adabwera kwa ophunzira ake nati, “Kodi monga mukugonabe ndi kupumula? Ndipotu nthaŵi ija yafika, Mwana wa Munthu akukaperekedwa kwa anthu ochimwa. Dzukani, tiyeni tizipita. Suuyu wodzandipereka uja, wafika.” Yesu akulankhula choncho, wafika Yudasi, mmodzi mwa ophunzira khumi ndi aŵiri aja. Adaabwera ndi khamu la anthu atatenga malupanga ndi zibonga. Anthuwo adaaŵatuma ndi akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda. Wodzampereka uja anali ataŵauza chizindikiro kuti, “Yemwe ndikamumpsompsoneyo, ndi ameneyo, mukamugwire.” Tsono Yudasi adadzangofikira pa Yesu, nkunena kuti, “Moni Aphunzitsi!” Atatero adamumpsompsona. Yesu adamuuza kuti, “Bwenzi langa, chita zimene wadzera.” Apo anthu aja adabwera namugwira Yesu. Koma wina mwa amene anali limodzi ndi Yesu, adasolola lupanga lake, natema wantchito wa mkulu wa ansembe onse, mpaka kumusenga khutu. Apo Yesu adamuuza kuti, “Bwezera lupangalo m'chimake, pakuti onse ogwira lupanga adzaphedwa ndi lupanga. Kodi ukuyesa kuti Ine sindingapemphe Atate, Iwo nthaŵi yomweyo nkunditumizira magulu ankhondo a angelo oposa khumi ndi aŵiri? Koma ndikadatero, nanga zikadachitika bwanji zimene Malembo adaneneratu kuti ziyenera kuchitika?” Pamenepo Yesu adaŵafunsa anthu aja kuti, “Bwanji mwachita kudzandigwira muli ndi malupanga ndi zibonga, ngati kuti ndine chigaŵenga? Tsiku ndi tsiku ndinkakhala pansi m'Nyumba ya Mulungu ndikuphunzitsa, inuyo osandigwira. Koma zonsezi zachitika kuti ziwonekedi zimene aneneri adalemba.” Pamenepo ophunzira ake onse aja adathaŵa, kumusiya yekha. Tsono anthu amene adagwira Yesu aja adapita naye kunyumba kwa Kayafa, mkulu wa ansembe onse. Kumeneko kudaasonkhana aphunzitsi a Malamulo ndi akulu a Ayuda. Koma Petro ankamutsatira chapatali, mpaka ku bwalo la nyumba ya mkulu wa ansembe uja. Adaloŵa m'kati, nakhala pansi pamodzi ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu kuti aone m'mene zithere. Akulu a ansembe aja ndi onse a m'Bwalo Lalikulu la Ayuda ankafunafuna umboni wonama woneneza Yesu kuti amuphe. Koma sadaupeze ngakhale padaabwera mboni zambiri zabodza. Potsiriza padabwera anthu aŵiri. Adati, “Munthu uyu ankati, ‘Ine ndingathe kupasula Nyumba ya Mulungu nkuimanganso pa masiku atatu.’ ” Tsono mkulu wa ansembe onse adaimirira nafunsa Yesu kuti, “Kodi ulibe poyankha? Nzotani zimene anthuŵa akukunenezazi?” Koma Yesu adangokhala chete. Pamenepo mkulu wa ansembe uja adauza Yesu kuti, “Ndikukulamula m'dzina la Mulungu wamoyo kuti utiwuze molumbira ngati ndiwedi Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu.” Yesu adamuyankha kuti, “Mwanena nokha. Komanso ndikukuuzani kuti kuyambira tsopano mudzaona Mwana wa Munthu atakhala ku dzanja lamanja la Mulungu wamphamvuzonse. Mudzamuwona akubwera pa mitambo.” Apo mkulu wa ansembe uja adang'amba zovala zake nati, “Kunyoza Mulungu koopsatu kumeneku! Kodi pamenepa nkufunanso mboni zina ngati? Mwadzimvera nokha kunyoza Mulungu koopsaku. Ndiye inu mukuganiza bwanji?” Iwo aja adayankha kuti, “Ayenera kuphedwa.” Pomwepo iwo adayamba kumthira malovu kumaso nkumamumenya, ena kumamuwomba makofi, nkumanena kuti, “Iwe Mpulumutsi wolonjezedwa uja, nanga sindiwe mneneri? Lota, wakumenya ndani?” Petro adaakhala kunja m'bwalo la nyumba ija. Mtsikana wina wantchito adabwera namuuza kuti, “Inunsotu munali ndi Yesu wa ku Nazareteyu.” Koma iye adakana pamaso pa anthu onse, adati, “Sindikuzidziŵa zimenezo ine.” Pamene Petro ankatuluka kumapita ku chipata, mtsikana winanso wantchito adamuwona, nayamba kuuza amene anali pamenepo kuti, “Akulu ameneŵa anali ndi Yesu wa ku Nazareteyu.” Petro adakananso molumbira kuti, “Ndithudi sindikumdziŵa munthu ameneyo.” Ndipo patangopita kanthaŵi, anthu amene anali pamenepo adadza nauza Petro kuti, “Ndithu nawenso ndiwe wa gulu lomweli, tadziŵira kalankhulidwe kakoka.” Apo Petro adayamba kulumbira nkumanena kuti, “Mulungu andilange, munthu mukunenayu ine sindimdziŵa konse.” Nthaŵi yomweyo tambala adalira. Tsono Petro adakumbukira mau aja a Yesu akuti, “Tambala asanalire, ukhala utakana katatu kuti sundidziŵa.” Pomwepo adatuluka, nakalira misozi ndi chisoni chachikulu. M'maŵa kutacha, akulu onse a ansembe ndi akulu a Ayuda adapanga upo kuti aphe Yesu. Adammanga, napita naye kwa Pilato, bwanamkubwa. Pamene Yudasi, wopereka Yesu kwa adani ake uja, adaona kuti Yesu mlandu wamuipira, nthumanzi idamugwira. Tsono adakaŵabwezera akulu a ansembe ndi akulu a Ayudawo ndalama makumi atatu zasiliva zija. Adati, “Ndidachimwa pakupereka munthu wosalakwa kuti aphedwe.” Koma iwo adati, “Ife tilibe nazo kanthu. Izo nzako.” Yudasi adakaziponya ndalamazo m'Nyumba ya Mulungu nachokapo, kenaka nkukadzikhweza. Akulu a ansembe aja adatola ndalamazo nati, “Malamulo athu satilola kuika ndalamazi m'bokosi la chuma cha m'Nyumba ya Mulungu, popeza kuti ndi za magazi.” Choncho adapangana kuti ndalamazo agulire munda wa mmisiri wa mbiya, kuti ukhale manda a alendo. Nchifukwa chake mpaka lero mundawo umatchedwa “Munda wa Magazi.” Motero zidapherezera zimene mneneri Yeremiya adaanena kuti, “Adatenga ndalama zija makumi atatu, mtengo wake umene Aisraele adaagamula, nagulira munda wa mmisiri wa mbiya, monga momwe Ambuye adaandilamulira.” Tsono Yesu adaimirira pamaso pa bwanamkubwa. Iyeyo adamufunsa kuti, “Kodi iwe, ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Yesu adati, “Mwanena nokha.” Koma pamene akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda aja ankamuneneza, Yesu sadayankhepo kanthu. Apo Pilato adamufunsa kuti, “Kodi sukumva zonse akukunenezazi?” Koma Yesu sadamuyankhe kanthu, kotero kuti bwanamkubwa uja adadabwa kwambiri. Pa nthaŵi ya chikondwerero cha Paska, bwanamkubwa ankaŵamasulira anthu mkaidi mmodzi, yemwe iwo ankafuna. Pa nthaŵi imeneyo panali mkaidi wina wodziŵika, dzina lake Barabasi. Tsono anthu atasonkhana, Pilato adaŵafunsa kuti, “Mukufuna kuti ndikumasulireni uti, Barabasi kapena Yesu, wotchedwa Khristu?” Adaatero chifukwa adaadziŵa kuti Yesuyo anthuwo angodzampereka chifukwa cha kaduka chabe. Pilato ali pa mpando woweruzira milandu, mkazi wake adamtumizira mau. Adati, “Musaloŵerepo pa nkhani ya munthu wolungamayo. Inetu maloto andivuta kwambiri usiku chifukwa cha Iyeyo.” Akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda adayamba kukakamiza anthu kupempha Pilato kuti amasule Barabasi, ndipo kuti Yesu aphedwe. Tsono bwanamkubwa uja adaŵafunsa kuti, “Mukufuna kuti ndikumasulireni uti mwa aŵiriŵa?” Anthu aja adati, “Barabasi.” Pilato adaŵafunsa kuti, “Nanga tsono ndichite naye chiyani Yesu, wotchedwa Khristuyu?” Anthu onse aja adati, “Apachikidwe pa mtanda!” Pilato adaŵafunsanso kuti, “Adalakwanji?” Koma anthu aja adafuula koposa kuti, “Apachikidwe pa mtanda!” Pilato adaona kuti sakuphulapo kanthu, ndipo kuti anthu ali pafupi kuchita chipwirikiti. Choncho adaitanitsa madzi, nkusamba m'manja pamaso pa anthu onse, nanena kuti, “Ine ndiye ndilibe kanthu pa imfa ya munthuyu. Izo nzanu.” Anthu onse aja adati, “Imfayo mlandu wake ugwere ife ndi ana athu.” Apo Pilato adaŵamasulira Barabasi, nalamula kuti Yesu akwapulidwe. Pambuyo pake adampereka kuti akampachike pa mtanda. Pamenepo asilikali a bwanamkubwa adatenga Yesu nakaloŵa naye kunyumba kwa bwanamkubwa. Adasonkhanitsa gulu lonse la asilikali anzao nazinga Yesu. Adamuvula zovala zake, namuveka chovala chofiira. Adaluka nsangamutu yaminga naiika pamutu pake, ndipo adamgwiritsa ndodo m'dzanja lake lamanja. Kenaka adayamba kumgwadira, namaseŵera naye mwachipongwe nkumanena kuti, “Tikuwoneni, mfumu ya Ayuda.” Adamthira malovu, natenga ndodo ija nkumamumenya nayo m'mutu. Ataseŵera naye mwachipongwe choncho, adamuvula chovala chija namuvekanso zovala zake. Kenaka adamtenga, nkupita naye kuti akampachike pa mtanda. Pamene ankatuluka mumzindamo, adakumana ndi munthu wina, dzina lake Simoni, wa ku Kirene. Tsono asilikali aja adamkakamiza kuti asenze mtanda wa Yesu. Ndipo adafika ku malo otchedwa Gologota, (ndiye kuti “Malo a Chibade cha Mutu.”) Kumeneko adapatsa Yesu vinyo wosanganiza ndi ndulu kuti amwe. Koma atalaŵa, adakana kumwa. Atampachika pa mtanda, adagaŵana zovala zake pakuchita maere. Kenaka adakhala pansi namamlonda. Pamwamba pa mutu wake adaalembapo mau osonyeza mlandu womuphera, akuti, “Uyu ndi Yesu, Mfumu ya Ayuda.” Adapachikanso pa mitanda zigaŵenga ziŵiri, china ku dzanja lamanja, china ku dzanja lamanzere. Anthu amene ankadutsa pamenepo, ankamunyodola nkumapukusa mitu. Ankanena kuti, “Iwe, suja unkati, ‘Ndidzapasula Nyumba ya Mulungu nkuimanganso pa masiku atatu?’ Ngati ndiwedi Mwana wa Mulungu tadzipulumutsatu nkutsika pamtandapo.” Nawonso akulu a ansembe pamodzi ndi aphunzitsi a Malamulo ndi akulu a Ayuda ankamuseka. Ankati, “Adapulumutsa anthu ena, koma akulephera kudzipulumutsa Iye mwini. Si Mfumu ya Aisraele nanga? Atsiketu tsopano pamtandapo kuti timkhulupirire. Ankadalira Mulungu; ampulumutsetu tsopano Mulunguyo, ngati amamkondadi; paja ankati, Ndine Mwana wa Mulungu!” Zigaŵenga zimene adaazipachika pamodzi ndi Yesu zija, nazonso zinkamunyoza chimodzimodzi. Kuyambira pa 12 koloko masana mpaka pa 3 koloko, padaagwa mdima pa dziko lonse. Tsono nthaŵi ili ngati 3 koloko, Yesu adafuula kwakukulu kuti, “Eli, Eli, lama sabakatani?” Ndiye kuti, “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?” Atamva mauwo, ena amene adaaimirira pamenepo adati, “Munthuyu akuitana Eliya.” Motero wina adathamanga nakatenga chinkhupule. Adachiviika m'vinyo wosasa, nkuchitsomeka ku bango nampatsira, kuti amwe. Koma ena adati, “Taima, tiwone ngati Eliya abweredi kudzampulumutsa.” Koma Yesu adafuulanso kwakukulu, napereka mzimu wake. Pompo chinsalu chochinga chija cha m'Nyumba ya Mulungu chidang'ambika pakatimpakati, kuyambira pamwamba mpaka pansi. Kudachita chivomezi, ndipo matanthwe adang'ambika. Manda adatsekuka ndipo anthu a Mulungu ambiri amene anali atamwalira kale, adauka kwa akufa. Adatuluka m'manda, ndipo Yesu atauka kwa akufa, iwo adaloŵa mu Yerusalemu, Mzinda Wopatulika, anthu ambiri nkumaŵaona. Mkulu wa asilikali ndiponso amene anali naye polonda Yesu, ataona chivomezi chija ndi zina zonse zimene zidaachitika, adachita mantha kwambiri nati, “Ndithudi, munthuyu adaalidi Mwana wa Mulungu.” Patali poteropo padaali azimai ambiri akungoyang'anitsitsa. Iwoŵa ndi amene adaatsatira Yesu kuchokera ku Galileya ndi kumamtumikira. Pakati pao panali Maria wa ku Magadala, Maria mai wa Yakobe ndi Yosefe, ndiponso mai wa ana a Zebedeo. Chisisira chitagwa, kudafika munthu wina wolemera, wochokera ku Arimatea, dzina lake Yosefe. Nayenso anali wophunzira wa Yesu. Iyeyu adakapempha mtembo wa Yesu kwa Pilato. Pilato adalamula kuti ampatse mtembowo. Tsono Yosefe adautenga, naukulunga m'nsalu yoyera yabafuta. Adakauika m'manda ake atsopano ochita chosema m'thanthwe. Tsono adagubuduzira chimwala pa khomo kuti atseke pamandapo, nachoka. Maria wa ku Magadala ndi Maria wina uja anali pomwepo atakhala pansi kuyang'anana ndi mandawo. M'maŵa mwake, litapita tsiku lokonzekera Sabata, akulu a ansembe pamodzi ndi Afarisi adasonkhana napita kwa Pilato. Adamuuza kuti, “Bwana, tikukumbukira kuti munthu wonyenga uja akali moyo ankati, ‘Patapita masiku atatu, ndidzaukanso.’ Tsono mulamule kuti azilondapo pamanda pake mpaka mkucha. Tikuwopa kuti ophunzira ake angadzabwere nkudzaba mtembo wake, kenaka namadzauza anthu kuti ‘Iye uja wauka kwa akufa.’ Apo kunyenga kotsirizaku kudzakhala koipa zedi kupambana koyamba kuja.” Pilato adaŵauza kuti, “Paja alonda muli nawo. Pitani, kalondeni pamandapo monga mukudziŵira.” Iwo adapitadi, nakatseka manda kolimba posindikiza chizindikiro pa chimwala chotsekeracho. Kenaka adasiya asilikali akulonda pomwepo. Tsiku la Sabata ya Ayuda litapita, Maria wa ku Magadala ndi Maria wina uja adabwera mbandakucha pa tsiku lotsatira Sabatalo, kudzaona manda aja. Mwadzidzidzi kudachita chivomezi chachikulu. Ndiye kuti mngelo wa Ambuye adaatsika kuchokera Kumwamba, nadzagubuduza chimwala chija, nkukhalapo. Maonekedwe ake anali ngati a mphezi, ndipo chovala chake chinali choyera chambee. Pamenepo alonda aja adachita mantha nayamba kunjenjemera, nkungoti gwa ngati anthu akufa. Koma mngeloyo adalankhula ndi azimai aja naŵauza kuti, “Inu musaope ai. Ndikudziŵa kuti mukufuna Yesu, uja adaampachika pa mtandayu. Sali muno ai, wauka monga muja adaaneneramu. Bwerani, dzaoneni pamene adaagona. Pitani msanga tsono, kauzeni ophunzira ake aja kuti, ‘Iye wauka kwa akufa, ndipo watsogolako kupita ku Galileya, mukamuwonera kumeneko.’ Kumbukirani zimene ndakuuzanizi.” Apo azimaiwo adachoka kumandako msanga, ali ndi mantha komanso ndi chimwemwe chachikulu, nathamanga kukauza ophunzira ake aja. Mwadzidzidzi Yesu adakumana nawo nati, “Monitu azimai!” Iwo adadza pafupi, nkugwira mapazi ake, nampembedza. Apo Yesu adaŵauza kuti, “Musaope. Pitani, kauzeni abale anga kuti apite ku Galileya. Akandiwonera kumeneko.” Pamene akazi aja ankapita, ena mwa alonda aja adakafika ku mzinda, nakasimbira akulu a ansembe zonse zimene zidaachitika. Tsono akulu a ansembe aja ndi akulu a Ayuda adasonkhana napangana nzeru. Adapatsa alonda aja ndalama zambiri, naŵauza kuti, “Muziti, ‘Ophunzira ake anabwera usiku nkuba mtembo wake ife tili m'tulo.’ Choncho bwanamkubwa akamva zimenezi, ife tidzamkhazika mtima pansi, ndipo sipadzakhala kanthu kokuvutani.” Alonda aja atalandira ndalama zija, adachitadi monga momwe adaaŵauzira. Motero mbiri imeneyi idawanda pakati pa Ayuda mpaka lero lino. Ophunzira khumi ndi mmodzi aja adapita ku Galileya kuphiri kumene Yesu adaapangana nawo kuti akakumane. Pamene adamuwona, adampembedza, koma ena ankakayika. Yesu adadza pafupi naŵauza kuti, “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pansi pano. Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera. Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.” Uwu ndi Uthenga Wabwino wonena za Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu. Udayamba monga mneneri Yesaya adalembera m'buku mwake kuti, “Mulungu akuti, “Ndidzatuma wamthenga wanga m'tsogolo mwako kuti akakonzeretu njira yoti iwe udzapitemo. Liwu la munthu wofuula m'chipululu: akunena kuti, ‘Konzani mseu wodzadzeramo Ambuye, ongolani njira zoti adzapitemo.’ ” Zimenezi zidachitikadi pamene Yohane Mbatizi adaafika ku chipululu, nayamba kulalika. Ankauza anthu kuti, “Tembenukani mtima, mubatizidwe, ndipo Mulungu adzakukhululukirani machimo anu.” Anthu ochokera ku dera lonse la Yudeya ndi a ku Yerusalemu ankadza kwa iye. Tsono ankati iwo akaulula machimo ao, iye nkumaŵabatiza mu Mtsinje wa Yordani. Yohaneyo ankavala zovala za ubweya wa ngamira, ndipo ankamangira lamba wachikopa m'chiwuno. Chakudya chake chidaali dzombe ndi uchi wam'thengo. Kulalika kwake ankati, “Pambuyo panga pakubwera wina wamphamvu kuposa ine, mwakuti ineyo ndine wosayenera ngakhale kuŵerama nkumasula zingwe za nsapato zake. Ine ndakubatizani ndi madzi, koma Iyeyo adzakubatizani mwa Mzimu Woyera.” Pa masiku amenewo Yesu adafika kuchokera ku Nazarete, mudzi wa ku Galileya, ndipo Yohane adambatiza mu mtsinje wa Yordani. Potuluka m'madzimo, adangoona kuthambo kukutsekuka, ndipo Mzimu Woyera akutsika pa Iye ngati nkhunda. Tsono kudamveka mau ochokera kumwamba akuti, “Iwe ndiwe Mwana wanga wapamtima. Ndimakondwera nawe kwambiri.” Nthaŵi yomweyo Mzimu Woyera adapititsa Yesu ku chipululu. Yesuyo adakhala kumeneko masiku makumi anai, Satana akumuyesa. Komweko kunalinso nyama zakuthengo, ndipo angelo ankamutumikira. Yohane uja ataponyedwa m'ndende, Yesu adapita ku Galileya akulalika Uthenga Wabwino wonena za Mulungu. Ankati, “Nthaŵi yakwana, Ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima ndi kukhulupirira Uthenga Wabwinowu.” Pamene Yesu ankayenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, adaona anthu aŵiri, Simoni ndi mbale wake Andrea, akuponya khoka m'nyanjamo, popeza kuti anali asodzi. Yesu adaŵauza kuti, “Inu, munditsate, ndikakusandutseni asodzi a anthu.” Pomwepo iwo adasiya makoka ao, namamtsatadi. Atapitirira pang'ono, Yesu adaona Yakobe ndi Yohane, ana a Zebedeo. Iwowo anali m'chombo, akukonza makoka ao, nthaŵi yomweyo Iye nkuŵaitana. Pamenepo iwowo adasiya bambo wao Zebedeo m'chombomo pamodzi ndi antchito ake, namatsata Yesu. Onsewo adapita ku Kapernao. Tsono litafika tsiku la Sabata, Yesu adaloŵa m'nyumba yamapemphero, nayamba kuphunzitsa. Zophunzitsa zake anthu zidaaŵagwira mtima kwambiri, chifukwa ankaphunzitsa moonetsa ulamuliro, kusiyana ndi m'mene ankachitira aphunzitsi a Malamulo. M'nyumba yamapempheroyo mudaaloŵa munthu wogwidwa ndi mzimu womuipitsa. Adalankhula mokuŵa kuti, “Kodi takuputani chiyani, Inu Yesu wa ku Nazarete? Kodi mwadzatiwononga? Ndakudziŵani, ndinu Woyera uja wa Mulungu.” Koma Yesu adazazira mzimu woipawo, adati, “Khala chete, tuluka mwa munthuyu.” Apo mzimu womuipitsa uja udamugwedeza kwamphamvu munthuyo, ndipo udakuwa koopsa, nkutuluka. Anthu onse aja adazizwa kwambiri, mpaka kumafunsana kuti, “Kodi zimenezi nzotani? Zophunzitsa zamtundutu zimenezi! Ngakhale mizimu yoipitsa anthu yomwe akuilamula ndi mphamvu, ndipo ikumumveradi.” Mwamsanga mbiri yake idawanda ponseponse ku dera lonse la ku Galileya. Pambuyo pake Yesu adachoka ku nyumba yamapemphero kuja, nakaloŵa pamodzi ndi Yakobe ndi Yohane m'nyumba ya Simoni ndi Andrea. Apongozi a Simoni anali gone, akudwala malungo, ndipo nthaŵi yomweyo anthu adamufotokozera za matendawo. Yesu adapita nakaŵagwira pa dzanja amaiwo nkuŵadzutsa, ndipo malungowo adatha. Pomwepo amai aja adayamba kukonzera anthu chakudya. Madzulo amenewo, dzuŵa litaloŵa, anthu adabwera kwa Yesu ndi anzao onse ovutika, ndi ogwidwa ndi mizimu yoipa. Anthu a m'mudzi monsemo adaasonkhana pakhomopo. Yesu adachiritsa ambiri amene ankavutika ndi matenda osiyanasiyana, ndipo adatulutsa mizimu yoipa yambiri. Koma mizimuyo ankailetsa kuti isalankhule, chifukwa idaamzindikira. M'mamaŵa ndithu, kusanache, Yesu adadzuka napita kumalo kosapitapita anthu. Kumeneko adakapemphera. Simoni ndi anzake aja adamlondola komweko. Atampeza adamuuza kuti, “Anthu onse akukufunafunani.” Koma Iye adaŵauza kuti, “Tiyeni tinke ku midzi ina kufupi konkuno, ndikalalike mau kumenekonso, pakuti ndizo ndidadzera.” Tsono adapita nalalika m'nyumba zamapemphero ku Galileya konseko, ndipo ankatulutsa mizimu yoipa. Munthu wina wakhate adadza kwa Yesu. Adamugwadira nayamba kumdandaulira. Adati, “Mutafuna, mungathe kundichiritsa.” Yesu adamumvera chifundo. Adatambalitsa dzanja nkumukhudza nati, “Chabwino, ndikufuna, chira!” Pomwepo khate lake lija lidatha, ndipo adachiradi. Tsono Yesu adamlamula kuti apite, namuuza mau amphamvu. Adati, “Chenjera, usakambire wina aliyense zimenezi. Ingopita, ukadziwonetse kwa wansembe, ndipo ukapereke nsembe adalamula Mose ija. Imeneyo ikhale yotsimikizira anthu onse kuti wachiradi.” Koma munthuyo atachoka pamenepo, adayamba kumaulula zonse, ndi kufalitsa nkhani imeneyi, kotero kuti Yesu sadathenso kuwonekera poyera m'mudzi uliwonse. Nchifukwa chake ankakhala kwina, kumalo kosapitapita anthu, koma anthu ankabwerabe kwa Iye kuchokera uku ndi uku. Patapita masiku pang'ono, Yesu adabwereranso ku Kapernao, anthu nkumva kuti ali kunyumba kwao. Anthu ochuluka adasonkhana m'nyumbamo, kotero kuti munalibenso malo ngakhale pakhomo pomwe. Iye ankaŵalalikira mau a Mulungu. Anthu ena anai adaanyamula munthu wa ziwalo zakufa, kubwera naye kwa Yesu. Koma sadathe kufika naye pafupi ndi Yesuyo chifukwa cha kuchuluka kwa anthu. Choncho adakwera pa denga, nangosasula dengalo kuyang'anana ndi pamene Yesu analiri, nkutsitsira pachiboopo machira amene adaanyamulira munthu uja. Poona chikhulupiriro chaocho, Yesu adauza munthu wa ziwalo zakufayo kuti, “Mwana wanga, machimo ako akhululukidwa.” Koma pamenepo panalinso aphunzitsi ena a Malamulo a Mose. Iwowo adayamba kudzifunsa mumtima mwao kuti, “Kodi Iyeyu angalankhule bwanji motere? Si kunyoza Mulungu kumeneku? Ndani angakhululukire machimo, si Mulungu yekha kodi?” Koma Yesu adaadziŵa kuti akuganiza zimenezi mumtima mwao, motero adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukuganiza zimenezo mumtima mwanu? Chapafupi koposa nchiti, kumuuza wa ziwalo zakufayu kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kunena kuti, ‘Dzuka, nyamula machira ako, yamba kuyenda?’ Koma kuti mudziŵe kuti Mwana wa Munthu ali nazo mphamvu pansi pano zokhululukira machimo, onani.” Pamenepo adauza wofa ziwalo uja kuti, “Iwe, dzuka, tenga machira ako, uzipita kumudzi.” Munthu uja adadzukadi, natenga machira ake aja nkutuluka, onse aja akuwona. Anthu onse aja adazizwa kwambiri, nayamba kutamanda Mulungu nkumanena kuti, “Zoterezi ife sitinaziwone nkale lonse.” Yesu adapitanso ku nyanja. Anthu ambirimbiri adafika komweko, ndipo Iye adayamba kuŵaphunzitsa. Pamene Yesu ankayenda, adaona Levi, mwana wa Alifeyo, ali pa ntchito m'nyumba ya msonkho. Adamuuza kuti, “Iwe, unditsate.” Iye adanyamuka nkumamutsatadi. Tsono pamene Yesu ankadya m'nyumba mwa Leviyo, panali anthu ambiri okhometsa msonkho ndi anthu ochimwa, odzadya nao ndi Yesuyo ndi ophunzira ake. Anali anthu ambiri ndithu amene adaatsagana naye. Pamene aphunzitsi a Malamulo a m'gulu la Afarisi adaona kuti Yesu akudya ndi anthu ochimwa, ndiponso ndi anthu okhometsa msonkho, adafunsa ophunzira ake kuti, “Bwanji akudya pamodzi ndi okhometsa msonkho ndiponso ndi anthu ochimwa?” Yesu atamva zimenezo adaŵayankha kuti, “Anthu amene ali bwino sasoŵa sing'anga ai, koma amene akudwala. Inetu sindidabwere kudzaitana anthu olungama, koma anthu ochimwa.” Nthaŵi ina ophunzira a Yohane Mbatizi ndiponso Afarisi ankasala zakudya. Anthu adadza kwa Yesu namufunsa kuti, “Kodi bwanji ophunzira a Yohane ndi ophunzira a Afarisi amasala zakudya, koma ophunzira anu ai?” Yesu adati, “Kani anzake a mkwati angathe kumasala zakudya pamene mkwati ali nao pomwepo? Chosatheka! Pamene mkwati ali nao pomwepo iwo sangamasale zakudya. Koma idzafika nthaŵi pamene adzaŵachotsere mkwatiyo. Pamenepo ndiye azidzasala zakudya. “Munthu satenga chigamba cha nsalu yatsopano nkuchisokerera pa chovala chakale. Chifukwa akatero, chigamba chatsopano chija chimakoka nkunyotsolako chovala chakalecho, ndiye kung'ambika kwake kumakhala kwakukulu koposa kale. Ndiponso munthu sathira vinyo watsopano m'matumba achikopa akale. Chifukwa akatero, vinyoyo amaphulitsa matumba aja, ndipo choncho vinyo uja amatayika, matumbawo nkutha ntchito. Koma vinyo watsopano amamuthira m'matumba atsopanonso.” Pa tsiku lina la Sabata Yesu ankadutsa m'minda ya tirigu. Akuyenda choncho, ophunzira ake adayamba kuthyolako ngala za tirigu nkumadya. Apo Afarisi adafunsa Yesu kuti, “Bwanji ophunzira anuŵa akuchita zimene siziloledwa pa tsiku la Sabata?” Iye adati, “Bwanji mukuchita ngati simudaŵerenge konse zimene adaachita Davide, pamene iye ndi anzake adaazingwa nayo njala? Suja adaaloŵa m'nyumba ya Mulungu, pa nthaŵi imene Abiyatara anali mkulu wa ansembe onse, nkukadya buledi woperekedwa kwa Mulungu? Chonsecho buledi ameneyo nkosaloledwa kuti wina aliyense nkumudya, kupatula ansembe okha. Komanso adaagaŵirako anzake aja amene adaali naye.” Tsono Yesu popitiriza mau, adauza Afarisiwo kuti, “Mulungu adaika tsiku la Sabata kuti likhale lothandiza anthu. Sadalenge anthu kuti akhale akapolo a tsiku la Sabata ai. Choncho Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro wonse pa zokhudza tsiku la Sabata.” Yesu adakaloŵanso m'nyumba yamapemphero. M'menemo mudaali munthu wina wopuwala dzanja. Anthu ena ankafuna chifukwa choti akamnenezere Yesuyo, motero ankangomuyang'anitsitsa kuti aone ngati achiritse munthuyo pa tsiku la Sabata. Yesu adalamula munthuyo kuti, “Imirira, bwera kutsogolo kuno.” Tsono adafunsa anthuwo kuti, “Kodi pa tsiku la Sabata chololedwa nchiti? Kuchitira anthu zabwino, kapena kuŵachita zoipa? Kupulumutsa moyo wa munthu, kapena kuuwononga?” Anthuwo adangoti chete. Pamenepo Yesu mtima wake udamuŵaŵa, poona kuti anali anthu okanika chotero, ndipo adaŵayang'ana ndi mkwiyo. Tsono adalamula munthuyo kuti, “Tambalitsa dzanja lako.” Iye adalitambalitsa, ndipo dzanja lakelo lidakhalanso bwino. Pamenepo Afarisi aja adatuluka nakachita upo ndi anthu a m'chipani cha Herode, kuti apangane njira yophera Yesu. Yesu pamodzi ndi ophunzira ake adachokapo napita ku Nyanja ya Galileya. Khamu lalikulu la anthu lidamtsatira. Anthu ake anali a ku Galileya, ena a ku Yudeya ndi ku Yerusalemu, ena a ku Idumeya, ndi kutsidya kwa Yordani, ndiponso kudera la ku Tiro ndi ku Sidoni. Onsewo adaafika kwa Iye, chifukwa anali atamva zimene Iye ankachita. Yesu adauza ophunzira ake kuti amuikire chombo pafupi, kuwopa kuti anthu angayambe kumpanikiza, chifukwa chidaali chikhamu chachikulu. Pakuti anali atachiritsa anthu ambiri, ndipo onse amene adaali ndi matenda ankakankhana pofuna kuti amkhudze. Mizimu yoipa inkati ikamuwona, inkadzigwetsa pansi pafupi ndi Iye nkumafuula kuti, “Inu ndinu Mwana wa Mulungu.” Koma Iye ankailetsa mwamphamvu kuti isamuulule. Yesu adakwera ku phiri, ndipo adaitana anthu amene Iye mwini ankaŵafuna, iwo nkupitadi kumene kunali Iyeko. Tsono adasankhapo khumi ndi aŵiri, naŵatcha dzina loti, “Atumwi.” Adaŵauza kuti, “Ndasankha inu kuti muzikhala nane, ndidzakutumani kukalalika, ndipo mudzakhala ndi mphamvu zotulutsira mizimu yoipa.” Anthu khumi ndi aŵiri amene adaaŵasankhawo ndi aŵa: Simoni (amene Yesu adamutcha dzina loti Petro), Yakobe ndi mbale wake Yohane, ana aja a Zebedeo (ameneŵa adaŵapatsa dzina lina lakuti Aboaneje, ndiye kuti “Oopsa ngati bingu”), Andrea ndi Filipo, kudza Bartolomeo, Mateyo, Tomasi, Yakobe (mwana wa Alifeyo), Tadeyo, Simoni (wa m'chipani chandale cha Azelote,) ndiponso Yudasi Iskariote (amene pambuyo pake adapereka Yesu kwa adani ake.) Pambuyo pake Yesu adapita kwao, ndipo anthu ambiri adasonkhananso, kotero kuti Iye ndi ophunzira ake analibe ndi mpata womwe wodyera chakudya. Achibale ake atamva zimenezi, adabwera kuti adzamtenge, chifukwa ankati, “Wachita misala.” Aphunzitsi ena a Malamulo, amene adaabwera kuchokera ku Yerusalemu, ankanena kuti, “Munthu ameneyu wagwidwa ndi Belezebulu.” Ankatinso, “Mphamvu zimene iyeyu amatulutsira mizimu yoipa nzochokera kwa mkulu wa mizimuyo.” Tsono Yesu adaitana anthu kuti adze pafupi, nanena mwafanizo kuti, “Kodi a mu ufumu wa Satana angathe bwanji kutulutsana okhaokha? Anthu a mu ufumu uliwonse akayamba kuukirana, ufumuwo sungalimbe. Ndipo anthu a m'banja limodzi akayamba kugaŵikana, banja lotere silingalimbe. Tsono ngati a mu ufumu wa Satana aukirana okhaokha nagaŵikana, Satanayo sangalimbe, ndiye kuti watha basi. “Wina sangathe kungoloŵa m'nyumba ya munthu wamphamvu nkumulanda katundu wake. Amayamba wammanga, kenaka ndiye kufunkha za m'nyumba mwakemo. “Ndithu ndikunenetsa kuti anthu angathe kukhululukidwa machimo onse, ngakhalenso zonena zao zonse zomunyoza Mulunguyo. Koma aliyense wonyoza Mzimu Woyera, sadzakhululukidwa konse. Tchimo lakelo limakhala mpaka muyaya.” Yesu adalankhula zimenezi poona kuti anthu aja ankanena kuti, “Wagwidwa ndi mzimu woipa.” Amai ake ndi abale ake a Yesu adabwera kunyumbako. Adaima panja, natuma anthu kuti akamuitane. Anthu ambirimbiri adaakhala pansi pomzungulira. Ndiye iwo aja adamuuza kuti, “Amai anu ndi abale anu ali panjapa, akukufunani.” Koma Iye adati, “Amai anga! Abale anga! Otinso?” Apo adayang'ana anthu amene anali pomzungulira aja nati, “Inetu amai anga ndi abale anga ndi aŵa. Aliyense wochita zimene Mulungu akufuna, ameneyo ndiye mbale wanga ndi mlongo wanga ndi amai anga.” Yesu adayambanso kuphunzitsa pambali pa Nyanja ya Galileya. Anthu ochuluka adasonkhana kumeneko, kotero kuti Iye adaayenera kuloŵa m'chombo, nakhala pansi m'menemo panyanjapo. Anthu onse adaakhala pansi pa mtunda m'mphepete mwa nyanjayo, ndipo Yesu adayamba kuŵaphunzitsa zambiri m'mafanizo. Poŵaphunzitsa adati, “Mvetsetsani! Munthu wina adapita kukafesa mbeu. Akufesa choncho, mbeu zina zidagwera m'njira, ndipo mbalame zidabwera nkuzitolatola. Mbeu zina zidagwera pa nthaka yamiyala, pamene panalibe dothi lambiri. Zidamera msanga, chifukwa nthakayo inali yosazama. Koma pamene dzuŵa lidakwera, zidapserera kenaka zidauma, chifukwa zinali zosazika mizu. Mbeu zina zidagwera pa zitsamba zaminga. Zitsambazo pokula zidalanda chakudya cha mbeu zija, kotero kuti mbeuzo sizidabereke konse. Koma mbeu zina zidagwera pa nthaka yabwino. Zidamera bwino nkukula, ndipo zidabereka. Ngala zina zinali ndi njere makumi atatu, zina makumi asanu ndi limodzi, zina makumi khumi.” Tsono Yesu adati, “Yemwe ali ndi makutu akumva, amve!” Pamene Yesu anali payekha, ophunzira khumi ndi aŵiri aja pamodzi ndi enanso amene ankakhala naye adadzamufunsa za mafanizowo. Iye adaŵayankha kuti, “Inuyo Mulungu adakuululirani zobisika zokhudza Ufumu wake. Koma enaŵa amene ali kunja, zonse amazimvera m'mafanizo chabe, kuti choncho, monga mau a Mulungu aja amanena, “ ‘Kuyang'ana ayang'ane ndithu, koma asapenye kanthu, ndipo kumva amve ndithu, koma asamvetse kanthu, kuti angatembenuke mtima, ndipo Mulungu angaŵakhululukire.’ ” Pambuyo pake Yesu adaŵafunsa kuti, “Monga simukulimvetsadi fanizo limeneli? Nanga mudzamvetsa bwanji fanizo lina lililonse? Wofesa mbeu uja ndi amene amafesa mau a Mulungu. Mbeu zogwera m'njira zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu. Koma nthaŵi yomweyo Satana amabwera, nkuchotsa mau aja amene adafesedwa m'mitima mwao. Mbeu zofesedwa pa nthaka yamiyala zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu, nthaŵi yomweyo nkuŵalandira ndi chimwemwe. Tsono popeza kuti mauwo sadazike mizu yozama, anthuwo amangolimbika kanthaŵi pang'ono chabe. Mwakuti pakangofika mavuto kapena masautso chifukwa cha mau aja, nthaŵi yomweyo anthuwo amabwerera m'mbuyo. Mbeu zofesedwa pa zitsamba za minga zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu. Koma kutanganidwa ndi zapansipano, kukondetsa chuma ndi kukhumba zinthu zina zambiri kumaloŵapo nkufooketsa mau aja, motero sabereka konse zipatso. Koma mbeu zofesedwa pa nthaka yabwino zija zikutanthauza anthu amene amamva mau a Mulungu, naŵalandira. Anthu otere amabereka zipatso, mwina makumi atatu, mwina makumi asanu ndi limodzi, mwina makumi khumi.” Tsono Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi anthu amatenga nyale nkuivundikira ndi mbiya, kapena kuibisa kunsi kwa bedi? Suja amaiika pa malo oonekera? Pajatu chinthu chilichonse chobisika chidzaululuka, ndipo chilichonse chachinsinsi chidzaonekera poyera. Yemwe ali ndi makutu akumva, amve!” Adaŵauzanso kuti, “Muzisamala pa mau amene mumamva. Muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu, ndipo inuyo adzakubzoletserani. Paja amene ali ndi kanthu kale, adzamuwonjezera zina. Koma amene alibe kanthu, ngakhale kamene ali nakoko adzamlandabe.” Yesu adaŵauzanso kuti, “Za Ufumu wa Mulungu tingazifanizire motere: munthu afesa mbeu m'munda. Iyeyo atha kumangogona usiku, m'maŵa nadzuka, nthaŵi yonseyo mbeu adafesa zija zikumera ndi kukula, mwiniwakeyo osadziŵa m'mene zonsezi zikuchitikira. Paja nthaka imabereketsa mbeuzo yokhayokha. Umayamba ndi mmera, kenaka ngala, pambuyo pake njere m'ngala muja zimakhwima. Tsono mbeuzo zikacha, munthu uja amatenga mpeni wodulira, pakuti nyengo yokolola yafika.” Yesu adatinso, “Kodi Ufumu wa Mulungu tingauyerekeze ndi chiyani? Kaya tiwufanizire ndi chiyani? Uli ngati njere ya mbeu ya mpiru. Pamene aifesa m'nthaka, ndi yaing'ono kwambiri mukaiyerekeza ndi njere zina pansi pano. Koma akaifesa, imamera, mbeu yake nkukula ndithu kupambana zitsamba zina zonse. Imachita nthambi zazikulu, kotero kuti mbalame zimatha kudzamanga zisa mumthunzi mwake.” Yesu ankaphunzitsa anthu ndi mafanizo ambiri onga ameneŵa, polinganiza ndi nzeru za anthuwo. Sankaŵaphunzitsa popanda mafanizo. Koma ankati akakhala payekha ndi ophunzira ake, ankaŵatanthauzira zonse. Tsiku lomwelo, dzuŵa litaloŵa, Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Tiyeni tiwoloke, tipite ku tsidya.” Tsono iwo adasiya khamu la anthu lija, natenga Yesu m'chombo momwe adaalimo. Padaalinso zombo zina zotsagana naye. Tsono padauka namondwe woopsa. Mafunde ankaloŵa m'chombomo, kotero kuti chidaayamba kudzaza ndi madzi. Koma nthaŵi imeneyo Yesu anali kumbuyo m'chombomo, ali m'tulo atatsamira mtsamiro. Pamenepo ophunzira aja adamudzutsa, adati, “Aphunzitsi, kodi simukusamalako kuti tikumira?” Yesu adadzuka, ndipo adadzudzula mphepoyo, nalamula nyanja kuti, “Tonthola! Khala bata!” Mphepo ija idalekadi, kenaka padagwa bata lalikulu. Apo Yesu adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukuchita mantha? Kani mulibe chikhulupiriro inu?” Koma iwo adaagwidwa ndi mantha kwambiri, nkumafunsana kuti, “Kodi Iyeyu ndi munthu wotani kuti ngakhale mphepo ndi nyanja zizimumvera?” Tsono Yesu ndi ophunzira ake adafika ku tsidya la Nyanja ya Galileya, ku dera la Agerasa. Yesu atangotuluka m'chombo, munthu wina wogwidwa ndi mzimu woipa adadzakumana naye kuchokera ku manda. Munthuyo ankakhala kumandako, ndipo padaalibe wina wothanso kummanga, ngakhale ndi unyolo womwe. Kale anthu adaayesa kangapo kummanga miyendo ndi zitsulo, ndiponso kummanga manja ndi maunyolo, koma iye ankangoŵamwetsula maunyolowo, ndipo zitsulo zomanga miyendozo ankangozithyola. Padaalibe ndi mmodzi yemwe wotha kumgonjetsa. Usana ndi usiku ankakhala kumandako ndi m'mapiri, akumangofuula ndi kudzipweteka ndi miyala. Pamene iye adaona Yesu chakutali, adamthamangira nadzamgwadira. Mokweza mau adati, “Kodi ndakuputani chiyani, Inu Yesu, Mwana wa Mulungu Wopambanazonse? M'dzina la Mulungu ndikukupemphani, musandizunze.” Adaatero chifukwa Yesu anali atanena kuti, “Mzimu woipawe, tuluka mwa munthuyu!” Tsono Yesu adamufunsa munthuyo kuti, “Dzina lako ndani?” Iye adayankha kuti, “Dzina langa ndine ‘Chigulu,’ chifukwa tilipo ochuluka.” Ndipo iye adadandaulira Yesu kwambiri kuti mizimuyo asaitulutsire kunja kwa dera limenelo. Pafupi pomwepo, pachitunda poteropo, pankadya gulu lalikulu la nkhumba. Tsono mizimu yoipa ija idapempha Yesu kuti, “Tipirikitsireni ku nkhumbazo, tiloleni tikaloŵe m'menemo.” Yesu adailoladi. Iyo idatuluka nkukaloŵadi m'nkhumbazo. Pomwepo gulu lonselo lidaguduka kutsika chitunda chija mwaliŵiro, nkukadziponya m'nyanja, mpaka kufera m'madzimo. Zonse zidaalipo ngati zikwi ziŵiri. Oŵeta nkhumbazo adathaŵa, nakasimbira anthu mu mzinda ndi ku midzi. Pamenepo anthu adatuluka kuti akaone zimene zidaachitikazo. Atafika kumene kunali Yesuko, adaona munthu adaagwidwa ndi mizimu yoipa uja atakhala pansi, atavala, misala ija itatha, munthu woti adaloŵedwa ndi chigulu cha mizimu yoipa. Anthuwo adagwidwa ndi mantha. Anzao amene adaaonerera zonse zikuchitika, adaŵasimbira zimene zidaamuchitikira munthu wamizimuyo ndiponso nkhumba zija. Apo anthuwo adampempha Yesu kuti achoke ku dera laolo. Pamene Yesu ankakaloŵa m'chombo, munthu amene adaagwidwa ndi mizimu yoipa uja adampempha kuti apite nao. Koma Yesu adakana namuuza kuti, “Iyai, iwe pita kumudzi kwa anthu akwanu, ukaŵafotokozere zazikulu zimene Ambuye akuchitira mwa chifundo chao.” Munthuyo adapitadi nakayamba kufalitsa ku dera lotchedwa Mizinda Khumi, zazikulu zimene Yesu adaamchitira. Atamva zimenezo anthu onse adazizwa kwambiri. Yesu adaolokanso nyanja. Pamene adafika pa tsidya, chinamtindi cha anthu chidasonkhana pamphepete pa nyanja pamene panali Iyepo. Tsono kudafika munthu wina, dzina lake Yairo, amene anali mmodzi mwa akulu a nyumba yamapemphero. Ataona Yesu, adadzigwetsa ku mapazi ake, nayamba kumdandaulira kwambiri. Adati, “Pepani, mwana wanga wamkazi ali pafupi kufa. Ngati nkotheka, mukamsanjike manja kuti achire ndi kukhala ndi moyo.” Yesu adanyamuka namapita naye. Anthu ambiri adatsagana naye namayenda momupanikiza. Tsono panali mai wina amene adakhala akuvutika ndi matenda a msambo pa zaka khumi ndi ziŵiri. Adaazunzika zedi ndi asing'anga ochuluka amene ankayesa kumuchiza. Mwakuti adaamwaza chuma chake chonse, komabe osapeza bwino konse. M'malo mwake matendawo analikunka nakulirakulira. Maiyo anali atamva za Yesu. Tsono adaloŵa m'chinamtindi cha anthu chija, nkuphaphatiza mpaka kukafika cha kumbuyo kwa Yesu, nakhudza chovala chake. Mumtima mwake ankaganiza kuti, “Ndikangokhudza ngakhale zovala zake zokhazo, ndichira.” Ndipodi nthaŵi yomweyo matenda a msambowo adaleka, mwiniwakeyo nkumva m'thupi mwake kuti matenda ake aja atha. Pomwepo Yesu adazindikira kuti mphamvu zina zatuluka mwa Iye. Tsono adatembenuka nayang'ana anthu aja ndipo adafunsa kuti, “Kodi ndani wandikhudza zovala?” Ophunzira ake adati, “Ndi Inu nomwe mukuwona kuti anthu akukupanikizani, ndiye mungafunse bwanji kuti, ‘Ndani wandikhudza?’ ” Koma Yesu adayang'anayang'ana kuti aone yemwe wachita zimenezo. Apo mai uja adachita mantha nayamba kunjenjemera, chifukwa anali atazindikira zimene zidaamuwonekerazo. Adadza pafupi, nadzigwetsa pansi pamaso pa Yesu, nkumufotokozera zonse monga momwe zidaachitikira. Yesu adamuuza kuti, “Inu mwana wanga, chikhulupiriro chanu chakuchiritsani. Pitani ndi mtendere. Matenda anu atheretu.” Yesu akulankhulabe, kudafika anthu kuchokera kunyumba kwa mkulu uja. Adamuuza mkuluyo kuti, “Mwana uja watsirizika. Musaŵavutenso Aphunzitsiŵa.” Koma Yesu sadasamale zimene anthuwo ankanena. Adauza mkulu uja kuti, “Musaope ai, inu mungokhulupirira.” Tsono sadalole kuti winanso atsagane naye, koma Petro, ndi Yakobe, ndi Yohane, mbale wa Yakobeyo. Pamene iwo adafika kunyumba kwa mkulu wa nyumba yamapemphero uja, Yesu adaona chipiringu cha anthu, akulira ndi kubuma. Iye ataloŵa, adaŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukuchita phokoso lonseli ndi kubuma? Mwanayutu sadamwalire ai, ali m'tulo chabe.” Pamenepo anthuwo adayamba kumseka monyodola. Iye adaŵatulutsira panja onse, nangotenga bambo wake ndi mai wake wa mwanayo, ndiponso amene adaali naye aja, nkuloŵa kuchipinda kumene kunali mwana uja. Tsono adagwira mwanayo pa dzanja namuuza kuti, “Talita, kumi.” (Ndiye kuti, “Mtsikana iwe, ndikuti dzuka.”) Pomwepo mtsikanayo adadzukadi, nayamba kuyenda, pakuti adaali wa zaka khumi ndi ziŵiri. Pamenepo anthu aja adazizwa kwambiri. Koma Yesu adaŵalamula mwamphamvu kuti zimenezo wina aliyense asazidziŵe. Kenaka adaŵauza kuti ampatse chakudya mtsikanayo. Yesu adachoka kumeneko, nakafika kumudzi kwao. Ophunzira ake adatsagana naye. Litafika tsiku la Sabata, Iye adayamba kuphunzitsa m'nyumba yamapemphero. Anthu ambiri amene ankamvetsera adadabwa kwambiri nkumanena kuti, “Kodi Iyeyu zonsezi adazitenga kuti? Nzeru zimene adalandirazi nzotani? Akutha bwanji kuchita zinthu zamphamvu zotere? Kodi ameneyu si mmisiri wa matabwa uja, mwana wa Maria? Kodi abale ake si Yakobe, ndi Yose, ndi Yudasi, ndi Simoni? Kodi suja alongo ake ali nafe pompano?” Choncho adakhumudwa naye. Koma Yesu adaŵauza kuti, “Mneneri amalemekezeka kwina kulikonse, kupatula kumudzi kwao, pakati pa achibale ake, ndiponso kubanja kwao.” Motero sadathe kuchita zinthu zamphamvu kumeneko. Adangosanjika manja pa odwala oŵerengeka, nkuŵachiritsa. Ndipo adadabwa poona kuti anthu akumeneko sadamkhulupirire. Pambuyo pake Yesu adapita ku midzi yozungulira, namakaphunzitsa anthu. Yesu adaitana ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja, naŵatuma aŵiriaŵiri. Adaŵapatsa mphamvu zotulutsira mizimu yoipitsa anthu. Adaŵalamula kuti, “Musatenge kanthu kena kalikonse pa ulendo, koma ndodo yokha. Musatenge kamba, kapena thumba lapaulendo, kapena ndalama m'chikwama. Nsapato muvale inde, koma musakhale ndi mikanjo iŵiri.” Adaŵauzanso kuti, “Mukafika pa mudzi, muzikhala nao kunyumba kumene mudafikirako, mpaka itakwana nthaŵi yoti muchoke kumudziko. Ngati kumudzi kwina anthu sakulandirani, nakana kumva mau anu, pochoka musanse fumbi la kumapazi kwanu. Chimenechi chidzakhala chizindikiro choti apalamula.” Ophunzira aja adapitadi, namakalalikira anthu kuti atembenuke mtima. Ankatulutsa mizimu yoipa yocholuka, ndiponso ankadzoza mafuta anthu odwala ambiri nkumaŵachiritsa. Mfumu Herode adaazimva zimenezi, pakuti mbiri ya Yesu inali itamveka ponseponse. Anthu ena ankati, “Yohane Mbatizi uja adauka kwa akufa, nkuwona akuchita zamphamvu zonsezi.” Koma ena ankati, “Iyai, ameneyu ndi Eliya.” Enanso ankati, “Iyai, koma ndi mneneri wonga aneneri akale aja.” Pamene Herode adamva zimenezi, adati, “Yohane yemwe ndidamdula pakhosi uja ndiye adauka kwa akufayu.” Pajatu Herode kale adaatuma asilikali ake kuti akagwire Yohane, akammange ndi kumponya m'ndende. Adaachita zimenezi chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa Filipo, mbale wake. Ndiye kuti Herode anali atamkwatira maiyo. Ndipo Yohane adaamuuza kuti, “Nkulakwira Malamulo kulanda mkazi wa mbale wanu.” Tsono Herodiasiyo ankadana naye Yohane, ndipo ankafuna kuti aphedwe basi. Koma ankalephera, chifukwa Herode ankaopa Yohane, podziŵa kuti anali munthu wolungama ndi woyera mtima. Choncho ankamusunga bwino. Ankakonda kumamvetsera mau ake, ngakhale kuti akamumva choncho, ankathedwa nzeru. Koma pa tsiku lokumbukira kubadwa kwa Herode, Herodiasi adapezerapo mwai. Herodeyo adakonza phwando, naitana akuluakulu a Boma, ndi akulu olamulira asilikali, ndi anthu omveka a ku Galileyako. Tsono mwana wamkazi wa Herodiasi adaloŵa, nayamba kuvina. Kuvinako adakondweretsa nako kwambiri Herode ndi amene adaali naye paphwandopo. Pamenepo mfumuyo idauza mtsikanayo kuti, “Undipemphe chilichonse chimene ukufuna, ine ndikupatsa.” Ndipo adatsimikiza molumbira kuti, “Chilichonse chomwe uti undipemphe, ndikupatsa ndithu, ngakhale kukudulira dziko langa lino pakati.” Mtsikanayo adatuluka nakafunsa mai wake kuti, “Kodi ndikapemphe chiyani?” Mai wakeyo adati “Kapemphe mutu wa Yohane Mbatizi.” Mtsikana uja adabwerera msanga kwa mfumu nanena kuti, “Ndifuna kuti tsopano pompano mundipatse mutu wa Yohane Mbatizi m'mbale.” Pamenepo mfumu Herode adamva chisoni kwambiri. Koma chifukwa cha malumbiro ake ndiponso chifukwa cha anthu oitanidwa ku phwando aja, sadafune kuphwanya lonjezo lake kwa mtsikanayo. Choncho nthaŵi yomweyo adatuma mmodzi mwa asilikali ake, namulamula kuti abwere nawo mutu wa Yohanewo. Msilikaliyo adapita ku ndende, nakamdula mutu Yohaneyo. Adaika mutu wakewo m'mbale nkubwera nawo, naupereka kwa mtsikana uja, mtsikanayo nkukaupereka kwa mai wake. Ophunzira a Yohane atamva zimenezi, adabwera nadzatenga mtembo wake nkukauika m'manda. Atumwi aja adabwerera kwa Yesu namufotokozera zonse zimene adaachita ndi kuphunzitsa. Yesu adaŵauza kuti, “Tiyeni tipite kwatokha kumalo kosapitapita anthu, kuti mukapumule pang'ono.” Adaatero chifukwa anthu anali piringupiringu, mwakuti iwo sankatha kupeza ndi mpata wodyera womwe. Tsono adaloŵa m'chombo napita kwaokha kumalo kosapitapita anthu. Komabe anthu ambiri adaŵaona akupita, naŵazindikira. Motero adathamanga pa mtunda kuchokera ku mizinda yonse, nakafika kumaloko, Yesu ndi ophunzira ake aja asanafike. Pamene Yesu adatuluka m'chombomo, adaona chikhamu chachikulu cha anthu. Adaŵamvera chifundo anthuwo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa, choncho adayamba kuŵaphunzitsa zambiri. Nthaŵi yamadzulo ophunzira ake adadzamuuza kuti, “Kunotu nkuthengo, ndipo ano ndi madzulo. Auzeni anthuŵa azipita, anke ku midzi ili pafupiyi kuti azikagula chakudya.” Koma Yesu adaŵauza kuti, “Inuyo apatseni chakudya.” Iwo adati, “Ndiyetu pafunika kuti tikagule buledi wa ndalama mazana aŵiri kuti tidzaŵadyetse anthu onseŵa!” Apo Yesu adaŵafunsa kuti, “Muli ndi buledi mngati? Takaonani.” Atakaona adati, “Alipo buledi msanu ndi nsomba ziŵiri.” Tsono Yesu adalamula kuti anthu onse aja akhale pansi m'magulumagulu pa msipu. Anthu aja adakhaladi pansi, m'magulu mwina anthu makumi khumi, mwina anthu makumi asanu. Yesu adatenga buledi msanu uja ndi nsomba ziŵiri zija, nayang'ana kumwamba, nkuthokoza Mulungu. Kenaka atanyemanyema bulediyo, adazipereka kwa ophunzira ake kuti akagaŵire anthuwo. Anthu onse aja adadya mpaka kukhuta. Pambuyo pake ophunzira aja adatola zotsala za buledi ndi za nsomba zija nkudzaza madengu khumi ndi aŵiri. Mwa anthu amene adaadya bulediyo amuna okha adaalipo zikwi zisanu. Madzulo omwewo Yesu adalamula ophunzira ake kuti aloŵe m'chombo, atsogole kunka ku tsidya la ku Betsaida, pamene Iye akuuza anthu kuti azipita kwao. Tsono atatsazikana nawo anthu aja, Iye adakwera ku phiri kukapemphera. M'mene kunkayamba kuda, nkuti chombo chija chili pakati pa nyanja, Yesu ali yekha pa mtunda. Ndiye adaona ophunzira aja akuvutika ndi kupalasa chombo, chifukwa anali atayang'anana ndi mphepo. M'mamaŵa kukali mbuu, Yesu adadza kwa iwo, Iye akuyenda pa madzi panyanjapo, nkumafuna kuŵapitirira. Koma ophunzira aja, pomuwona akuyenda pa madzi, adaaganiza kuti ndi mzukwa, nayamba kukuwa. Onsewotu atamuwona adaaopsedwa. Koma nthaŵi yomweyo Yesu adaŵauza kuti, “Khazikani mtima pansi, ndine, musaope.” Pamenepo adaloŵa m'chombomo, mphepo nkuleka. Iwowo adathedwa nzeru kwabasi, chifukwa anali asanamvetse bwino za buledi zija. Mitu yao idaali youma. Yesu ndi ophunzira ake adaoloka nyanja, nakafika ku Genesarete, nkuimitsa chombo kumeneko. Pamene iwo adatuluka m'chombomo, nthaŵi yomweyo anthu adamzindikira Yesu. Adathamangira ku midzi ya kufupi ndi kumeneko, nayamba kumabwera ndi anthu odwala pa machira, kudza nawo kumene ankamva kuti Yesu ali uku. Kulikonse kumene Yesu ankapita, ku midzi ndi ku mizinda, anthu ankadzakhazika odwala pa mabwalo. Ankamupempha kuti aŵalole odwalawo kungokhudza ngakhale mphonje ya chovala chake. Mwakuti onse amene ankaikhudza, ankachira. Tsiku lina Afarisi ena pamodzi ndi aphunzitsi ena a Malamulo, amene adaachokera ku Yerusalemu, adasonkhana kwa Yesu. Iwo adaaona kuti ophunzira ake ena ankangodya chakudya osasamba m'manja moyenera (ndiye kuti mosasamala mwambo wosamba m'manja.) Pajatu Afarisi ndi Ayuda ena onse saadya asanasambe m'manja mwa njira yoyenera. Amatero kuti asunge mwambo wa makolo. Ndipo akachokera ku msika, saadya osasamba m'manja. Amasunganso miyambo ina yambiri imene makolo ao adaŵasiyira, monga kutsuka zikho, miphika, ndi ziŵiya zamkuŵa [ndi mabedinso.] Choncho Afarisi ndi aphunzitsi a Malamulo aja adamufunsa Yesu kuti, “Chifukwa chiyani ophunzira anu sasunga mwambo wa makolo, koma amangodya chakudya osasamba m'manja moyenera?” Yesu adaŵayankha kuti, “Inu anthu achiphamaso, ndithu mneneri Yesaya adaanenadi zoona muja adaalemba kuti, “ ‘Anthu aŵa amangondilemekeza ndi pakamwa chabe, koma mtima wao uli kutalitali ndi Ine. Amandipembedza inde, koma kupembedza kwaoko nkopanda phindu, chifukwa zimene amaphunzitsa ngati zophunzitsa zenizeni, ndi malamulo a anthu chabe.’ ” Kenaka Yesu adati, “Inu mumasiya Malamulo a Mulungu, nkumasunga miyambo ya anthu.” Tsono popitiriza mau, Yesu adati, “Koma ndiye muli ndi njira yanu yochenjera yosiyira Malamulo a Mulungu kuti musunge miyambo yanu. Paja Mose adalamula kuti, ‘Lemekeza atate ako ndi amai ako,’ ndiponso kuti, ‘Wonyoza atate ake kapena amai ake, aziphedwa basi.’ Koma inu mumati, ‘Munthu akauza atate ake kapena amai ake kuti, “Zimene ndikadakuthandiza nazoni zasanduka Korobani,” (ndiye kuti zoperekedwa kwa Mulungu), ameneyo sasoŵanso kuŵathandiza atate ake ndi amai ake.’ Pakutero mau a Mulungu inu mumaŵasandutsa achabechabe, chifukwa cha mwambo wanu umene mumasiyirana. Ndipo mumachita zinanso zambiri zotere.” Pambuyo pake Yesu adaitananso anthu aja kuti adze pafupi, ndipo adaŵauza kuti, “Mverani nonsenu, ndipo mumvetse bwino. Palibe chinthu chochokera kunja ndi kuloŵa m'kati mwa munthu chimene chingathe kumuipitsa. Koma zimene zimatuluka mwa munthu ndizo zimamuipitsa.” [ “Yemwe ali ndi makutu akumva, amve!”] Pamene Yesu adasiya khamu lija la anthu nakaloŵa m'nyumba, ophunzira ake adamufunsa za fanizo limeneli. Iye adaŵayankha kuti, “Kani ngakhale inunso simumvetsa? Kodi simukudziŵa kuti chilichonse chochokera kunja, ndi kuloŵa mwa munthu, sichingathe kumuipitsa? Pajatu sichiloŵa mumtima mwake, koma m'mimba, pambuyo pake nkumakatayidwa ku thengo.” (Pakunena zimenezi, Yesu adagamula kuti zakudya zonse anthu angathe kuzidya.) Adatinso, “Zimene zimatuluka mwa munthu, ndizo zimamuipitsa. Chifukwa m'kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, za chiwerewere, za kuba, za kuphana, zigololo, masiriro, kuipa mtima, kunyenga, zonyansa, kaduka, kunyoza, kudzikuza, ndiponso kupusa. Zoipa zonsezi zimachokera m'kati mwa munthu, ndipo ndizo zimamuipitsa.” Yesu adanyamuka kupita ku dera la ku Tiro. Adakakhala kunyumba kwina, ndipo sadafune kuti anthu adziŵe kuti ali kumeneko. Komabe sadathe kubisika. Nthaŵi yomweyo mai wina, amene mwana wake wamkazi ankavutika ndi mzimu woipa, adamva za Iye. Adabwera kwa Yesu nagwada kumapazi kwake. Maiyo anali mkunja, wa mtundu wa anthu a ku Siro-Fenisiya. Adapempha Yesu kuti akatulutse mzimu woipawo mwa mwana wake. Koma Yesu adamuyankha kuti, “Ai, alekeni ana ayambe adya nkukhuta. Sibwino kutenga chakudya cha ana nkuponyera agalu.” Apo maiyo adati, “Nzoonadi, Ambuye, koma suja ngakhale agalu omwe amakhala m'munsi mwa tebulo nkumadyako nyenyeswa zimene ataya ana?” Apo Yesu adamuuza kuti, “Chifukwa cha mau mwanenaŵa, pitani, mzimu woipawo watuluka mwa mwana wanu.” Mai uja adabwerera kunyumba kwake, nakapezadi mwanayo ali gone pa bedi, mzimu woipa uja utatuluka. Yesu adachokanso ku dera lija la ku Tiro, namayenda kudutsa dera la ku Sidoni, kupita ku nyanja ya ku Galileya, kudzera pakati pa dera la Mizinda Khumi. Anthu ena adabwera kwa Iye ndi munthu yemwe anali gonthi ndi wolankhula movutikira. Anthuwo adapempha Yesu kuti amchiritse pomusanjika manja munthuyo. Yesu adatengera munthu uja pambali kumchotsa pa khamu la anthu. Adapisa zala m'makutu a munthuyo, nalavula malovu, nkukhudza lilime la munthu uja. Adayang'ana kumwamba, nadzuma, nkumuuza kuti, “Efata!” ndiye kuti “Tsekuka!” Pomwepo makutu a munthuyo adatsekuka, ndipo chimene chinkamanga lilime lake chidamasuka, mpaka adayamba kulankhula bwino lomwe. Yesu adalamula anzake a munthuyo kuti, “Musakauzetu wina aliyense zimenezi.” Koma ngakhale adaŵaletsa mwamphamvu choncho, iwo adanka nalengeza ndithu zimenezi. Ndipo anthu adazizwa kopitirira ndithu. Adati, “Ameneyu amachita zonse bwino. Ngakhale agonthi amaŵachiritsa nkumamva, ndipo osalankhula amaŵalankhulitsa.” Pasanapite nthaŵi yaitali anthu ambirimbiri adasonkhananso. Pamene Yesu adaona kuti anthuwo alibe chakudya, adaitana ophunzira ake naŵauza kuti, “Ndikuŵamvera chifundo anthuŵa, chifukwa akhala nane masiku atatu tsopano, ndipo alibe chakudya. Ndikangoŵabweza kwao ali ndi njala chonchi, alefuka pa njira, chifukwa ena achokera kutali.” Ophunzira ake adamufunsa kuti, “Anthu ochuluka chotereŵa munthu angaŵapezere bwanji chakudya chokwanira, kuthengo ngati kuno?” Yesu adaŵafunsa kuti, “Buledi ndiye muli naye mngati?” Iwo aja adati, “Msanu ndi muŵiri.” Apo Yesu adalamula anthu aja kuti akhale pansi. Kenaka adatenga buledi msanu ndi muŵiri uja, adathokoza Mulungu, namunyemanyema nkumupereka kwa ophunzira ake kuti akagaŵire anthu aja. Ophunzira aja adaŵagaŵiradi anthuwo. Adaalinso ndi tinsomba toŵerengeka. Yesu adathokoza Mulungu chifukwa cha tinsombato, nalamula ophunzira ake kuti atiperekenso kwa anthu aja. Anthu adadya mpaka kukhuta. Adatola zotsala, nadzaza madengu asanu ndi aŵiri. Anthu amene adaali pamenepo, amuna okha adaalipo ngati zikwi zinai. Pambuyo pake Yesu adatsazikana nawo anthu aja, kenaka Iye ndi ophunzira ake adaloŵa m'chombo napita ku dera la Dalamanuta. Tsiku lina kudabwera Afarisi ena, nayamba kutsutsana ndi Yesu. Iwo adaapempha Yesu kuti aŵaonetse chizindikiro chozizwitsa chochokera kumwamba. Pakutero ankangofuna kumutchera msampha. Yesu adadzumira mu mtima nati, “Kodi bwanji anthu a mbadwo uno amafuna kuwona chizindikiro chozizwitsa? Ndithu ndikunenetsa kuti anthu a mbadwo unowu sadzachiwona chizindikiro akufunacho.” Atatero, Yesu adaŵasiya, naloŵanso m'chombo kuwolokera ku tsidya lina. Ophunzira a Yesu anali ataiŵala kutenga buledi, kotero kuti m'chombomo adaali ndi buledi mmodzi yekha. Tsono Yesu adayamba kuŵalangiza kuti, “Muchenjere nacho chofufumitsira buledi cha Afarisi ndi cha Herode.” Apo ophunzirawo adayamba kukambirana nkumati, “Akuterotu chifukwa tilibe buledi.” Yesu adaadziŵa zimene iwo ankanena. Ndiye adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukukambirana zakuti mulibe buledi? Kodi mpaka pano simunazindikirebe kapena kumvetsa? Kani mitu yanu ndi youma, eti? Maso muli nawo, kodi simuwona? Ndipo makutu muli nawo, kodi simumva? Kodi inu simukukumbukira zijazi? Muja ndidaanyemanyema buledi msanu kuti ndidyetse anthu zikwi zisanumu, kodi mudaadzaza madengu angati a zotsala?” Ophunzirawo adati, “Madengu khumi ndi aŵiri.” Yesu adaŵafunsanso kuti, “Nanga muja ndidaanyemanyema buledi msanu ndi muŵiri ndi kudyetsa anthu zikwi zinaimu, mudaatola madengu angati a zotsala?” Iwo adati, “Madengu asanu ndi aŵiri.” Apo Yesu adati, “Nanga ndiye simunamvetsebe?” Yesu ndi ophunzira ake adafika ku Betsaida. Kumeneko anthu adabwera ndi munthu wakhungu, napempha Yesu kuti amchiritse pomkhudza. Yesu adamgwira dzanja, natuluka naye kunja kwa mudzi. Adapaka malovu m'maso mwa munthuyo, namsanjika manja nkumufunsa kuti, “Kodi ukuwona kanthu?” Munthu uja adaŵeramuka nati, “Ndikuwona anthu akuyenda, koma akuwoneka ngati mitengo.” Yesu adamuikanso manja kumaso kwake. Munthu uja adayang'anitsitsa ndipo adachira, nayamba kumapenya zonse bwino lomwe. Yesu adamuuza kuti apite kwao, namlamula kuti, “Usaloŵe ndi m'mudzi momwemu.” Yesu ndi ophunzira ake adapita ku midzi ya ku Kesareya-Filipi. Pa njira Yesu adafunsa ophunzira akewo kuti, “Kodi anthu amati Ine ndine yani?” Iwo adayankha kuti, “Ena amati ndinu Yohane Mbatizi, ena amati ndinu Eliya, enanso amati ndinu mmodzi mwa aneneri.” Apo Yesu adaŵafunsa kuti, “Nanga inuyo, mumati ndine yani?” Petro adamuyankha kuti, “Inu ndinu Mpulumutsi wolonjezedwa uja.” Yesu adaŵalamula kuti asauze munthu wina aliyense za Iye. Yesu adayamba kuphunzitsa ophunzira ake kuti, “Mwana wa Munthu adzayenera kuzunzidwa kwambiri. Akulu a Ayuda, ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo adzamkana. Iye adzaphedwa, koma patapita masiku atatu adzauka.” Zimenezi adazinena mosabisa konse. Apo Petro adamtengera pambali, nayamba kumdzudzula. Koma Yesu adacheuka, nayang'ana ophunzira ake ena aja, ndipo adadzudzula Petro. Adati, “Choka apa, iwe Satana! Maganizo akoŵa si maganizo a Mulungu ai, ndi maganizo a anthu chabe.” Pambuyo pake Yesu adaitana khamu la anthu pamodzi ndi ophunzira aja kuti adze pafupi naye, ndipo adaŵauza kuti, “Munthu wofuna kutsana Ine, adzikane mwiniwakeyo, ndipo asenze mtanda wake nkumanditsata. Chifukwa wofuna kupulumutsa moyo wake, adzautaya, koma wotaya moyo wake chifukwa cha Ine ndi Uthenga Wabwino, adzaupulumutsa. Nanga ndiye kuti munthu wapindulanji atapata zonse za pansi pano, iyeyo nkutaya moyo wake? Munthu angalipire chiyani choti aombolere moyo wake? Tsono ngati munthu achita manyazi ndi Ine ndiponso ndi mau anga pamaso pa anthu ochimwa a makonoŵa amene ali osakhulupirika, ameneyo nanenso Mwana wa Munthune ndidzachita naye manyazi pamene ndidzabwera pamodzi ndi angelo oyera, ndili ndi ulemerero wa Atate anga.” Yesu adaŵauzanso kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti alipo ena pompano omwe sadzafa asanaone Ufumu wa Mulungu utafika ndi mphamvu.” Patapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu adatenga Petro ndi Yakobe ndi Yohane, nakwera nawo ku phiri lalitali, kwaokha. Tsono maonekedwe a Yesu adasinthika iwo akuwona. Zovala zake zidasanduka zoŵala ndi zoyera kuti mbee, kupambana m'mene mmisiri wina aliyense angayeretsere nsalu pansi pano. Nthaŵi yomweyo ophunzira aja adaona Eliya ndi Mose, akukambirana ndi Yesu. Petro adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, ndi bwino kuti ife tili nao pano. Tiloleni timange misasa itatu, wina wanu, wina wa Mose, wina wa Eliya.” Ankatero chifukwa chosoŵa chonena, pakuti iye ndi anzake aja anali atagwidwa ndi mantha aakulu. Tsono padafika mtambo, nuŵaphimba, ndipo mumtambomo mudamveka mau akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimamkonda, muzimumvera.”? Mwadzidzidzi ophunzirawo poyang'anayang'ana, adangoona kuti palibenso wina amene anali nawo pamenepo, koma Yesu yekha. Pamene ankatsika phirilo, Yesu adaŵaletsa kuti zimene adaaonazo asauze wina aliyense mpaka Mwana wa Munthu atauka kwa akufa. Iwo adasungadi chinsinsichi, koma ankafunsana okhaokha kuti, “Kodi kuuka kwa akufa akunena Yesuku ndiye kuti chiyani?” Tsono adamufunsa kuti, “Nanga bwanji aphunzitsi a Malamulo amati Eliya adzayenera kuyamba wabwera?” Yesu adaŵayankha kuti, “Zoonadi, Eliya adzayambadi wabwera, kuti adzakonzenso zonse. Komabe bwanji Malembo amanena kuti Mwana wa Munthu adzayenera kuzunzidwa kwambiri ndi kunyozedwa? Ine ndikukuuzani kuti Eliya adafikadi, ndipo anthu adamchita zonse zomwe iwo ankafuna, monga momwe Malembo adaanenera za iye.” Pamene Yesu ndi ophunzira atatuwo adabwerera kwa ophunzira ena aja, adapeza chikhamu chachikulu cha anthu chitaŵazinga. Aphunzitsi a Malamulo ankatsutsana ndi ophunzirawo. Pamene anthu onsewo adaona Yesu, adadabwa kwambiri, ndipo adamthamangira kudzamlonjera. Iye adaŵafunsa kuti, “Kodi mukutsutsana zotani?” Mmodzi mwa anthuwo adayankha kuti, “Aphunzitsi, ine ndinabwera ndi mwana wanga wamwamuna kuti ndidzampereke kwa Inu, chifukwa adaloŵedwa ndi mzimu woipa womuletsa kulankhula. Umati ukangomugwira, umamgwetsa pansi, mwanayo nkumangoti thovu tututu kukamwa, namakukuta mano, mpaka thupi gwagwagwa kuuma. Ndiye ndinapempha ophunzira anuŵa kuti autulutse, koma alephera.” Apo Yesu adati, “Ha! Anthu a mbadwo wopanda chikhulupiriro! Ndiyenera kukhala nanube mpaka liti? Ndiyenera kukupirirani mpaka liti? Tabwera nayeni kuno mwanayo.” Adabwera nayedi. Mzimu woipa uja utangoona Yesu, nthaŵi yomweyo wayamba kumzunguza mwamphamvu mnyamata uja, mpaka iye pansi khu, nkumangovimvinizika, thovu lili tututu kukamwa. Yesu adafunsa bambo wake uja kuti, “Kodi zimenezi zidamuyamba liti?” Bambo wakeyo adati, “Zidamuyamba ali mwana ndithu. Mzimu umenewu wakhala ukumugwetsa kaŵirikaŵiri, mwina amagwa pa moto, mwina m'madzi, kufuna kumupha. Koma ngati Inu mungathe kuchitapo kanthu, chonde tatichitirani chifundo, mutithandize.” Yesu adati, “Bwanji mukuti, ‘Ngati mungathe?’ Zinthu zonse nzotheka kwa amene ali ndi chikhulupiriro.” Pomwepo bambo wa mwana uja adanena mokweza mau kuti, “Ndikukhulupirira, koma mpang'ono chabe. Thandizeni kuti ndikhulupirire kwenikweni.” Pamene Yesu adaona kuti chikhamu cha anthu chija chayamba kupanikizana pamenepo, adazazira mzimu woipawo, adati, “Iwe mzimu woletsa kulankhula ndi kumva, ndikukulamula kuti utuluke mwa mwanayu, ndipo usadzaloŵenso mwa iye.” Mzimuwo udafuula numzunguza mwamphamvu mwana uja, kenaka nkutuluka. Mwanayo adangoti zii ngati wafa, mpaka ambiri nkumati, “Watsirizika basi!” Koma Yesu adamugwira dzanja namdzutsa, mwanayo nkuimirira. Yesu atakaloŵa m'nyumba, ophunzira ake adamufunsa ali paokha, kuti, “Ifeyo ndiye tinalephera bwanji kuutulutsa mzimu woipa uja?” Yesu adayankha kuti, “Mzimu wa mtundu umenewu, pokhapokha mutayamba mwapemphera mpamene mungautulutse.” Atachoka kumeneko, Yesu ndi ophunzira ake ankadutsa m'dziko la Galileya. Koma Iye sadafune kuti anthu adziŵe, chifukwa ankaphunzitsa ophunzira ake. Ankaŵauza kuti, “Mwana wa Munthu akudzaperekedwa kwa anthu, ndipo iwowo adzamupha. Koma atamupha, Iye adzauka patapita masiku atatu.” Ophunzira ake sadamvetse mau ameneŵa, komabe ankaopa kumufunsa. Yesu ndi ophunzira ake adafika ku Kapernao. Ataloŵa m'nyumba, Iye adaŵafunsa kuti, “Kodi panjira paja mumatsutsana zotani?” Ophunzirawo adangoti chete. Ndiye kuti zimene ankatsutsana panjirapo zinali zakuti wamkulu ndani pakati pao. Yesu adakhala pansi, naŵaitana ophunzira khumi ndi aŵiri aja. Ndipo adaŵauza kuti, “Ngati wina afuna kukhala wamkulu, adzisandutse wamng'ono, wotumikira onse.” Atatero adatenga mwana, namkhazika pakati pao nkumufungata, naŵauza kuti, “Aliyense wolandira bwino mwana wonga ngati uyu chifukwa cha Ine, ndiye kuti akulandira bwino Ine amene. Ndipo wondilandira Ine bwino, ndiye kuti akulandira bwino osati Ineyo, koma Atate amene adandituma.” Yohane adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, ife tinaona munthu wina akutulutsa mizimu yoipa potchula dzina lanu, ndiye ife tinayesa kumletsa chifukwa sayenda nafe.” Koma Yesu adati, “Musamletse ai, chifukwa munthu sangati atachita zamphamvu m'dzina langa, nthaŵi yomweyo nkundinyoza. Chifukwa wosatsutsana nafe, ndi wogwirizana nafe ameneyo. Aliyense amene akupatsani chikho cha madzi chifukwa chakuti ndinu ake a Khristu, ndithu ndikunenetsa kuti ameneyo sadzalephera kulandira mphotho yake.” “Aliyense wochimwitsa ngakhale mmodzi mwa ana okhulupirira Ineŵa, ameneyo kukadakhala kwabwino koposa kuti ammangirire chimwala cha mphero m'khosi ndi kukamuponya m'nyanja. Tsono ngati dzanja lako likuchimwitsa, lidule. Ndi bwino kuti ukaloŵe ku moyo wosatha uli woduka dzanja, kupambana kuti ukaloŵe uli ndi manja onse aŵiri ku Gehena, kwa moto wosazimika.” [ “Kumeneko mphutsi zoŵazunza sizifa, moto wakenso woŵatentha suzima.”] “Ngati phazi lako likuchimwitsa, lidule. Ndi bwino kuti ukaloŵe ku moyo wosatha uli woduka phazi, kupambana kuti ukaponyedwe ku Gehena uli ndi miyendo yonse iŵiri.” [ “Kumeneko mphutsi zoŵazunza sizifa, moto wakenso woŵatentha suzima.”] “Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, likolowole. Ndi bwino kuti ukaloŵe mu Ufumu wa Mulungu uli ndi diso limodzi lokha, kupambana kuti akakuponye ku Gehena uli ndi maso onse aŵiri. Kumeneko mphutsi zoŵazunza sizifa, moto wakenso woŵatentha suzima. “Onse adzayeretsedwa ndi moto monga momwe nsembe imayeretsedwa ndi mchere. Mchere ndi wabwino, koma ngati mcherewo watha mphamvu, mphamvu zakezo nkuzibwezeranso nchiyani? Moyo wanu ukhale ngati wothiridwa mchere, ndipo muzikhala ndi mtendere pakati panu.” Yesu adachoka ku Kapernao, napita ku dera la ku Yudeya ndi ku dera la kutsidya kwa mtsinje wa Yordani. Anthu ambirimbiri adadzasonkhananso kwa Iye, ndipo monga ankazoloŵera, adayambanso kuŵaphunzitsa. Tsono kudafika Afarisi ena, namufunsa kuti, “Kodi nkololedwa kuti munthu asudzule mkazi wake?” Pomufunsa chonchi ankangofuna pomupezera chifukwa. Koma Yesu poyankha adati, “Kodi Mose adakulamulani zotani?” Iwo adati, “Mose adalola kuti munthu azilembera mkazi wake kalata yachisudzulo kenaka nkumuchotsa.” Yesu adati, “Mose adaakulemberani lamulo limeneli chifukwa cha kukanika kwanuku. Komatu pachiyambi paja, pamene Mulungu adalenga zonse, adaŵalenga anthu, wina wamwamuna wina wamkazi. Nchifukwa chake mwamuna azisiya atate ndi amai, nakaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo aŵiriwo adzasanduka thupi limodzi. Choncho tsopano salinso aŵiri, koma thupi limodzi. Tsono zimene Mulungu wazilumikiza pamodzi, munthu asazilekanitse.” Pamene adaloŵanso m'nyumba, ophunzira adamufunsanso Yesu za nkhani yomweyi. Iye adaŵauza kuti, “Aliyense amene asudzula mkazi wake nakwatira wina, akuchita chigololo, ndipo akumchimwira mkazi wakeyo. Chimodzimodzinso ngati mkazi asudzula mwamuna wake, kenaka nkukwatiwa ndi wina, nayenso akuchita chigololo.” Anthu ena ankabwera ndi ana kwa Yesu kuti aŵakhudze ndi kuŵadalitsa, ophunzira ake nkumaŵazazira. Yesu ataona zimenezi, adakalipa naŵauza kuti, “Alekeni anaŵa azibwera kwa Ine, musaŵaletse. Paja Ufumu wa Mulungu ndi wa anthu otere. Ndithu ndikunenetsa kuti yemwe salandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana, ameneyo sadzaloŵamo.” Atatero adayamba kuŵafungata anawo, naŵasanjika manja ndi kuŵadalitsa. Pamene Yesu ankanyamuka kuti azipita, munthu wina adamthamangira. Adadzamugwadira namufunsa kuti, “Aphunzitsi abwino, kodi ndizichita chiyani kuti ndikalandire moyo wosatha?” Yesu adamuyankha kuti, “Ukunditchuliranji wabwino? Wabwinotu ndi mmodzi yekha, Mulungu basi. Malamulo ukuŵadziŵa: Usaphe, usachite chigololo, usabe, usachite umboni wonama, usadyerere mnzako, lemekeza atate ako ndi amai ako.” Munthu uja adati, “Aphunzitsi, zonsezi ndakhala ndikuzitsata kuyambira ndili mwana.” Yesu atamuyang'ana, adamkonda nkumuuza kuti, “Ukusoŵabe chinthu chimodzi: pita, kagulitse zonse zimene uli nazo. Ndalama zake ukapatse anthu osauka, ndipo chuma udzachipeza Kumwamba. Kenaka ubwere, uzidzanditsata.” Atamva zimenezo, munthu uja nkhope yake idagwa, adangochokapo ali wovutika mu mtima, chifukwa adaali munthu wa chuma chambiri. Yesu adayang'ana ophunzira ake amene adaamzungulira naŵauza kuti, “Nkwapatali kwambiri kwa anthu achuma kuti akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.” Ophunzirawo adadabwa nawo kwambiri mau akeŵa. Koma Yesu adabwerezanso, adati, “Ndithu, inu ana anga, nkwapatali kukaloŵa mu Ufumu wa Mulungu. Nkwapafupi kuti ngamira idzere pa kachiboo ka zingano, kupambana kuti munthu wachuma akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.” Pamenepo ophunzira aja adazizwa koposa, nayamba kufunsana kuti, “Tsono nanga angathe kupulumuka ndani?” Yesu adaŵayang'ana nati, “Kwa anthu nkosathekadi, koma ndi Mulungu ai, nkotheka. Paja ndi Mulungu zonse nzotheka.” Pamenepo Petro adayamba kulankhula naye, adati, “Ifetu paja tidasiya zonse kuti tizikutsatani.” Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti aliyense wosiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amai, kapena atate, kapena ana, kapena minda chifukwa cha Ine, ndiponso chifukwa cha Uthenga Wabwino, ameneyo pansi pompano adzalandira zonsezo mochuluka kwambiri koposa kale: nyumba, abale, alongo, amai, ana, minda, komanso mazunzo. Ndipo kutsogoloko adzalandira moyo wosatha. Komatu ambiri amene ali oyambirira adzakhala otsirizira, ndipo amene ali otsirizira adzakhala oyambirira.” Pamene iwo anali pa ulendo wopita ku Yerusalemu, Yesu ankayenda patsogolo pa ophunzira ake. Ophunzirawo anali oda nkhaŵa kwambiri. Ndipo anthu amene ankaŵatsatira anali ndi mantha. Yesu adaŵaitaniranso pambali ophunzira khumi ndi aŵiri aja, nayamba kuŵafotokozera zimene zinalikudzamugwera. Adati, “Tilitu pa ulendo wa ku Yerusalemu. Kumeneko Mwana wa Munthu akukaperekedwa kwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo. Iwo akamuweruza ndi kugamula kuti aphedwe. Ndipo akampereka kwa anthu akunja. Amenewo akamchita chipongwe, akamthira malovu, akamkwapula nkumupha. Koma patapita masiku atatu, Iye adzauka.” Yakobe ndi Yohane, ana aja a Zebedeo, adadzauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, ife timati bwanji titakupemphani kanthu, mutichitire.” Yesu adaŵafunsa kuti, “Inuyo mukufuna kuti ndikuchitireni chiyani?” Iwo adati, “Timafuna kuti pamene mudzakhale mu ulemerero wanu, mudzatiike wina ku dzanja lanu lamanja, wina ku dzanja lanu lamanzere.” Koma Yesu adati, “Simukudziŵa zimene mukupempha. Kodi inu mungathe kumwa nao chikho chamasautso chimene ndikudzamwera Ine? Kodi inu mungathe kulandira nao ubatizo wa mavuto umene ndikudzalandira Ine?” Iwo aja adayankha kuti, “Inde, tingathe.” Apo Yesu adati, “Chabwino, chikho chimene Ine ndikudzamwacho, inunso mudzamwa nao, ndipo ubatizo umene Ine ndikudzalandirawo, inunso mudzalandira nao. Koma Ineyo si udindo wanga kusankha munthu kuti akhale ku dzanja langa lamanja, kapena ku dzanja langa lamanzere. Mulungu ndiye adzapereke malo ameneŵa kwa omwe Iye mwini adaŵakonzera.” Pamene khumi ena aja adamva zimenezi, adapsera mtima Yakobeyo ndi Yohaneyo. Koma Yesu adaŵaitana ophunzira akewo, naŵauza kuti, “Mukudziŵa kuti pakati pa anthu akunja, anthu amene amati ngolamulira, amadyera anthu ao masuku pa mutu. Akuluakulu aonso amaonetsadi mphamvu zao pa anthu ao. Koma pakati pa inu zisamatero ai. Aliyense wofuna kukhala mkulu pakati panu, azikhala mtumiki wanu. Ndipo aliyense wofuna kukhala mtsogoleri pakati panu, azikhala kapolo wa onse. Chitani monga m'mene adachitira Mwana wa Munthu: adabwera osati kuti ena adzamtumikire ai, koma kuti Iyeyo adzatumikire anthu ndi kupereka moyo wake kuti aombole anthu ochuluka.” Yesu ndi ophunzira ake pamodzi ndi gulu lalikulu la anthu adafika ku mzinda wa Yeriko. Tsono pamene ankatuluka mumzindamo, adapeza wakhungu wina wopemphapempha atakhala pansi pamphepete pa mseu. Munthuyo dzina lake anali Baratimeo, mwana wa Timeo. Tsono iyeyo atamva kuti ndi Yesu wa ku Nazarete, adayamba kufuula kuti, “Inu Yesu, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo.” Anthu ambiri adamzazira kuti akhale chete. Koma iye adafuulirafuulira kuti, “Inu Mwana wa Davide, mundichitire chifundo.” Yesu adaima, nauza anthu kuti, “Tamuitanani.” Anthu aja adamuitana wakhunguyo namuuza kuti, “Limba mtima, nyamuka, akukuitana.” Pomwepo iye uja adadzambatuka, mwinjiro wake uko chi, kuthamangira kwa Yesu. Yesu adamufunsa kuti, “Kodi ukufuna kuti ndikuchitire chiyani?” Wakhunguyo adayankha kuti, “Mbuyanga, ndikufuna kuti ndizipenyanso.” Yesu adamuuza kuti, “Chabwino, ungathe kupita, chikhulupiriro chako chakuchiritsa.” Nthaŵi yomweyo adayambadi kupenya, nkumatsata Yesu pa ulendowo. Pamene Yesu ndi ophunzira ake ankayandikira ku Yerusalemu, kufupi ndi ku Betefage ndi Betaniya, midzi ya ku Phiri la Olivi, Iye adatuma aŵiri mwa ophunzirawo, naŵauza kuti, “Pitani m'mudzi mukuwonawo. Mukangoloŵamo, mukapeza mwanawabulu ali chimangire, amene munthu sanakwerepo chikhalire. Mukammasule nkubwera naye. Wina akakakufunsani kuti, ‘Inu, nchiyani chimenecho?’ Inu mukati, ‘Ambuye ali naye ntchito, akangothana naye amtumiza konkuno nthaŵi yomweyo.’ ” Ophunzira aja adapitadi, nakapeza mwanawabuluyo ali chimangirire pa khomo m'mbali mwa mseu, ndipo adayamba kummasula. Anthu amene adaali pamenepo adaŵafunsa kuti, “Inu nchiyani chimenecho, buluyo mukummasuliranji?” Ophunzirawo adaŵayankha monga momwe adaaŵauzira Yesu. Tsono anthuwo adaŵalola kuti ammasule. Ophunzira aja adabwera naye mwanawabuluyo kwa Yesu. Adayala zovala zao pamsana pa bulu uja, Yesu nkukwerapo. Anthu ambiri ankayala zovala zao mu mseu, ena nkumayalika nthambi zamasamba zomwe ankakazithyola ku thengo. Anthu amene adaali patsogolo, ndi amene adaali m'mbuyo, adayamba kufuula kuti, “Ulemu kwa Mulungu. Ngwodala amene alikudza m'dzina la Ambuye. Udalitsidwe Ufumu wa atate athu Davide umene ulikudza tsopano. Ulemu kwa Mulungu kumwambamwamba.” Yesu ataloŵa m'Yerusalemu, adakaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, nayang'anayang'ana zonse. Tsono poti chisisira chinali chitagwa, adatuluka napita ku Betaniya pamodzi ndi ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja. M'maŵa mwake, pamene iwo ankachoka ku Betaniya kuja, Yesu adaamva njala. Ataona mkuyu chapatali potero, uli ndi masamba, adapitapo kuti kapena nkupezamo nkhuyu. Koma atafika, sadapezemo nkhuyu, koma masamba okhaokha, pakuti siinali nyengo ya nkhuyu. Pamenepo adauza mtengowo kuti, “Mtengo iwe, kuyambira tsopano mpaka muyaya wina aliyense asadzadyekonso zipatso zako.” Mau ameneŵa ophunzira ake aja adaŵamva. Iwo adafika ku Yerusalemu. Tsono Yesu adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, nayamba kutulutsa anthu amene ankachita malonda m'menemo. Adagubudula matebulo a osinthitsa ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda. Sadalolenso kuti wina aliyense azidutsa m'mabwalo a Nyumbayo atasenza chinthu ai. Pambuyo pake adayamba kuŵaphunzitsa naŵauza kuti, “Paja Malembo akuti, ‘Nyumba yanga idzatchedwa Nyumba yopemphereramo anthu a mitundu yonse.’ Koma inu mwaisandutsa phanga la achifwamba.” Akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo atamva zimenezi, adayamba kufunafuna njira yoti amuphere. Pakutitu ankachita naye mantha poona kuti anthu onse ankadabwa nazo zimene Iye ankaphunzitsa. Kutayamba kuda, Yesu ndi ophunzira ake adatulukamo mumzindamo. M'maŵa mwake, m'mamaŵa ndithu, iwo akuyenda mu mseu, adaona mkuyu uja waumiratu wonse ndi mizu yomwe. Apo Petro adakumbuka zijazi, ndipo adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, taonani, mkuyu uja mudautembererawu wauma.” Yesu adaŵayankha kuti, “Muzikhala ndi chikhulupiriro mwa Mulungu. Ndithu ndikunenetsa kuti aliyense wolamula phiri ili kuti, ‘Choka apa, kadziponye m'nyanja,’ atanena ndi mtima wosakayika, nakhulupirira ndithu kuti zimene akunenazo zichitikadi, ndithu zidzachitikadi monga momwe waneneramo. Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti, m'mapemphero mwanu mukapempha Mulungu chinthu chilichonse, muzikhulupirira kuti mwalandira, ndipo mudzachilandiradi. Ndipo pamene mukuti mupemphere, muziyamba mwakhululukira mnzanu ngati muli naye nkanthu. Mukatero, Atate anunso amene ali Kumwamba adzakukhululukirani machimo anu.” [ “Koma ngati inu simukhululukira anzanu, Atate anunso amene ali Kumwamba sadzakhululukira machimo anu.”] Yesu adafikanso ku Yerusalemu. Tsono pamene Iye ankangodziyendera m'Nyumba ya Mulungu, akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo pamodzi ndi akulu a Ayuda adadzamufunsa kuti, “Kodi mphamvu zoti muzichita zimenezi mudazitenga kuti? Ndani adakupatsani mphamvu zimenezi?” Yesu adati, “Nanenso ntakufunsani funso limodzi. Mukandiyankha, ndiye ndikuuzeni kumene ndidatenga mphamvu zoti ndizichita zimenezi. Kodi Yohane kuti azibatiza, mphamvu zake adaazitenga kwa yani, kwa Mulungu kapena kwa anthu? Tandiyankhani.” Iwo aja adayamba kukambirana nkumati, “Tikati adaazitenga kwa Mulungu, Iyeyu anena kuti, ‘Nanga bwanji tsono simudamkhulupirire?’ Komanso tikati adaazitenga kwa anthu, apo ndiye ainso.” Adaatero chifukwa choopa anthu, pakuti anthu onse ankati Yohane anali mneneri weniweni. Ndiye adangomuyankha Yesuyo kuti, “Kaya, ife sitikudziŵa.” Apo Iye adati, “Nanenso tsono sindikuuzani kumene ndidazitenga mphamvu zoti ndizichita zimenezi.” Yesu adayamba kulankhula nawo m'mafanizo. Adati, “Munthu wina adaabzala mipesa m'munda mwake, namanga mpanda kuzinga mundawo. Adakumba nkhuti yoponderamo mphesa, namanga nsanja yolondera mundawo. Pambuyo pake munda uja adaubwereka alimi, iye nkunyamuka ulendo wa ku dziko lina. Nyengo yothyola zipatso itafika, munthu uja adatuma wantchito wake kwa alimi aja, kuti alimiwo akampatsireko zipatso za m'munda muja. Koma alimiwo adamugwira wantchitoyo nammenya, nkumubweza osampatsa kanthu. Munthu uja adatumanso wantchito wina, koma alimi aja adamtema m'mutu nkumunyazitsa. Munthuyo adatumanso wantchito wina, uyu ndiye adangomupheratu. Adachita chimodzimodzi ndi antchito ena ambiri, ena adaŵamenya, ena kuŵapheratu. “Munthu uja adangotsala ndi mmodzi basi, mwana wake weniweni wapamtima. Ndiye pambuyo pa onse adadzatuma iyeyu. Adati, ‘Mwana wanga yekhayu akamchitira ulemu.’ Koma alimi aja adayamba kuuzana kuti, ‘Ameneyu ndiye amene ati adzamsiyire chumachi. Tiyeni timuphe kuti chidzakhale chathu.’ Tsono adamugwiradi, namupha nkumuponya kunja kwa mundawo. “Kodi mwini munda wamphesa uja adzachita chiyani? Ndithu, adzabwera naŵapha alimiwo, munda uja nkuubwereka alimi ena. Nanga monga simudaŵerenge Malembo aja akuti, “ ‘Mwala umene amisiri omanga nyumba adaaukana, womwewo wasanduka mwala wapangondya, wofunika koposa. Ambuye Mulungu ndiwo adachita zimenezi, ndipo nzotidabwitsa kwambiri.’ ” Pamene akulu a Ayuda aja adazindikira kuti fanizolo Yesu ankaphera iwowo, adafunitsitsa kumugwira, koma ankaopa khamu la anthu. Tsono adangomusiya nachokapo. Anthu ena a m'gulu la Afarisi, ndi enanso a m'chipani cha Herode, adaatumidwa kuti akatape Yesu m'kamwa. Atafika, adati, “Aphunzitsi, tikudziŵa kuti Inu mumanena zoona, ndipo simuwopa munthu aliyense. Simuyang'anira kuti uyu ndani, koma mumaphunzitsa malamulo a Mulungu moona. Nanga tsono, kodi Malamulo a Mulungu amalola kuti tizikhoma msonkho kwa Mfumu ya ku Roma, kapena ai? Kodi tizikhomadi kapena tisamakhoma?” Koma Yesu podziŵa maganizo ao onyenga, adati, “Bwanji kodi mukundiyesa dala? Tandipatsirani ndalama, ntaiwona.” Iwo adampatsadi ndalamayo. Tsono Iye adaŵafunsa kuti, “Kodi nkhopeyi ndi ya yani, ndipo dzinali ndi la yani?” Iwo aja adati, “Zonse ndi za Mfumu ya ku Roma.” Apo Yesu adaŵauza kuti, “Tsono perekani kwa Mfumu zake za Mfumuyo, ndiponso kwa Mulungu zake za Mulunguyo.” Atamva zimenezi anthuwo adathedwa nzeru. Pambuyo pake Asaduki ena adadza kwa Yesu. Iwo amati akufa sadzauka. Adamufunsa kuti, “Aphunzitsi, Mose adatilembera lamulo lakuti, ‘Ngati munthu amwalira, nasiya mkazi, koma opanda ana, mbale wake wa womwalirayo aloŵe chokolo, kuti amuberekere ana mbale wake uja.’ Tsono padaali anthu asanu ndi aŵiri pachibale pao. Woyamba adaakwatira mkazi, namwalira opanda mwana. Wachiŵiri adamtenga mai uja, nayenso nkumwalira osasiya mwana. Wachitatunso chimodzimodzi. Mpaka asanu ndi aŵiri onse aja adamwalira osasiya mwana. Potsiriza pake mai uja nayenso adamwalira. Nanga tsono pa tsiku lodzauka akufa, mwini mkaziyo adzakhala utiwuti, popeza kuti abale asanu ndi aŵiri onse aja adaamkwatirapo?” Yesu adaŵayankha kuti, “Si pamenepa nanga pomwe mumalakwira, chifukwa chosadziŵa Malembo ndiponso mphamvu za Mulungu? Pajatu pouka akufa, palibenso za kukwatira kapena kukwatiwa ai. Onse ali ngati angelo Kumwamba. Tsono zakuti anthu adzauka kwa akufa, kodi simudaŵerenge m'buku la Mose, paja akunena za chitsamba choyakapa? Suja akuti Mulungu adamuuza Mose kuti, ‘Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, ndine Mulungu wa Isaki, ndine Mulungu wa Yakobe?’ Ndiye kutitu sali Mulungu wa anthu akufa ai, koma wa anthu amoyo. Inu ndinu olakwa kwabasi.” Mphunzitsi wina wa Malamulo adaŵamva akutsutsana. Ataona kuti Yesu waŵayankha bwino Asaduki aja, adadza pafupi, namufunsa kuti, “Kodi mwa malamulo onse, lalikulu ndi liti?” Yesu adamuyankha kuti, “Lamulo lalikulu ndi ili, ‘Tamverani, inu Aisraele, Chauta, Mulungu wathu, Iye yekha ndiye Mulungu. Motero, uzikonda Chauta, Mulungu wakoyo, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu zako zonse.’ Lamulo lachiŵiri lake ndi ili, ‘Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.’ Palibe lamulo lina loposa malamulo ameneŵa.” Mphunzitsi wa Malamulo uja adati, “Ai, mwayankha bwino, Aphunzitsi. Monga mwaneneramo, nzoonadi kuti Mulungu ndi mmodzi yekhayo, ndipo palibe winanso koma Iye yekha. Mwalondolanso ponena kuti chinthu chopambana ndicho kumkonda Mulungu ndi mtima wonse, ndi nzeru zonse, ndi mphamvu zonse, ndiponso kukonda mnzako monga umadzikondera iwe wemwe. Kuteroko nkoposa kupereka nsembe zopsereza ndiponso nsembe zina zonse.” Yesu adaona kuti munthuyo wayankha mwanzeru. Tsono adamuuza kuti, “Iwe suli kutali ndi Ufumu wa Mulungu.” Ndipo kuyambira apo panalibenso wina woti ayesere kumfunsa kanthu. Pamene Yesu ankaphunzitsa anthu m'Nyumba ya Mulungu, adafunsa kuti, “Kodi bwanji aphunzitsi a Malamulo amati Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndi mwana wa Davide? Paja Davide, ndi nzeru zochokera kwa Mzimu Woyera, adati, “ ‘Chauta adauza Mbuye wanga kuti, Khala ku dzanja langa lamanja, mpaka nditasandutsa adani ako kuti akhale ngati chopondapo mapazi ako.’ Davide weniweniyo akutchula Mpulumutsi wolonjezedwa uja kuti Mbuye wake. Tsono angakhale mwana wakenso bwanji?” Anthu ambirimbiri aja ankakondwa kwambiri pomva mau ake. Pamene Yesu ankaŵaphunzitsa, adati, “Chenjera nawoni aphunzitsi a Malamulo. Amakonda kuyenda atavala mikanjo yaitali, ndi kuti anthu aziŵalonjera mwaulemu pa misika. Amakonda mipando yaulemu kwambiri m'nyumba zamapemphero, ndiponso malo olemekezeka pa maphwando. Koma amaŵadyera chuma chao azimai amasiye, nkumapemphera mapemphero ataliatali monyengezera. Anthu ameneŵa adzalangidwa koposa.” Tsiku lina Yesu adaakhala pansi kuyang'anana ndi bokosi loponyamo ndalama zopereka ku Nyumba ya Mulungu. Ankayang'anitsitsa m'mene anthu ankaponyera ndalama zao. Anthu ambiri achuma ankaponyamo ndalama zambiri. Koma padafika mai wina wamasiye, wosauka. Iyeyu adangoponyamo tindalama tiŵiri. Tsono Yesu adaitana ophunzira ake naŵauza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti mai wamasiye wosaukayu waponyamo koposa anthu ena onseŵa, amene akuponya ndalama m'bokosimu. Chifukwa ena onseŵa angoponyamo zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo. Koma maiyu, mwa umphaŵi wake, waponyamo zonse zimene anali nazo, ngakhale zimene akadagulira chakudya.” Pamene Yesu ankachoka ku Nyumba ya Mulungu, wophunzira wake wina adamuuza kuti, “Aphunzitsi, taonani kukongola kwake miyalayi ndi nyumbazi.” Yesu adamuuza kuti, “Kodi mukuziwona nyumba zikuluzikuluzi? Sipadzatsala konse mwala ndi umodzi womwe pamwamba pa mwala unzake: yonse adzaigumula.” Pambuyo pake Yesu adakhala pansi, pa Phiri la Olivi, kuyang'anana ndi Nyumba ya Mulungu. Tsono Petro, Yakobe, Yohane ndi Andrea adamufunsa paokha, kuti, “Tatiuzani bwino, zimenezi zidzachitika liti? Tidzaonera chiyani kuti zonsezi zili pafupi kuchitika?” Yesu adayamba kuŵauza kuti, “Chenjerani kuti wina aliyense asadzakusokezeni. Chifukwa kudzafika anthu ambiri m'dzina langa namadzanena kuti, ‘Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndine,’ ndipo adzasokeza anthu ambiri. Koma inu mukadzamva phokoso la nkhondo za kufupi kuno, kapena mphekesera za nkhondo zakutali, musadzade nkhaŵa ai. Zimenezi zidzayenera kuchitika, koma sindiye kuti chimalizo chija chafika kale ai. Mitundu yosiyanasiyana idzaukirana, maiko osiyanasiyana adzamenyana nkhondo. Kudzachita zivomezi ku malo osiyanasiyana, ndipo kudzakhala njala. Tsono zonsezitu nkuyamba chabe kwa mavuto. “Koma inu muchenjere. Anthu adzakuperekani ku mabwalo amilandu a Ayuda, ndipo adzakukwapulani m'nyumba zao zamapemphero. Mudzaonekera kwa akulu a Boma ndi kwa mafumu chifukwa cha Ine, kuti mukandichitire umboni pamaso pao. Nkofunika kuti Uthenga Wabwino uyambe walalikidwa kwa anthu a mitundu yonse. Tsono akadzakugwirani ndi kukuperekani ku mlandu, musadzaderetu nkhaŵa nkumaganiza kuti, ‘Kodi tikanene chiyani?’ Ai, inu mukangonena zimene Mulungu akakuuzeni pa nthaŵi imeneyo. Pajatu odzalankhula sindinu ai, koma Mzimu Woyera. Mbale azidzapereka mbale wake kuti aphedwe, bambo azidzapereka mwana wake. Ana azidzaukira makolo ao, mpaka kuŵaphetsa. Anthu onse adzadana nanu chifukwa cha Ine. Koma yemwe adzalimbikire mpaka potsiriza, ameneyo ndiye adzapulumuke.” “Chosakaza chonyansa chija chidzakhala atachiimika pamalo pomwe sichiyenera kukhalapo. (Umvetse bwino amene ukuŵerengawe.) Mukadzaona zimenezi, pamenepo amene ali m'Yudeya adzathaŵire ku mapiri. Amene ali padenga pa nyumba yake, asati atsike kuti akatenge chinthu m'nyumba mwakemo. Yemwe ali ku munda, asabwererenso ku nyumba kuti akatenge mwinjiro. Ali ndi tsoka akazi amene adzakhale ndi pathupi, ndiponso azimai oyamwitsa ana masiku amenewo. Pempherani kuti zimenezi zisadzaoneke pa nyengo yachisanu, chifukwa masautso amene adzaoneke masiku amenewo, sanaonekepo chilengedwere dziko lapansi mpaka pano, ndipo sadzaonekanso. Tsonotu masiku amenewo, Ambuye akadapanda kuŵachepetsa, sakadapulumukapo munthu ndi mmodzi yemwe. Koma masikuwo Mulungu adaŵachepetsa chifukwa cha anthu omwe Iye adaŵasankha. “Pa nthaŵi imeneyo, wina akadzakuuzani kuti, ‘Ali panotu Khristu uja,’ kapena kuti, ‘Uyo ali apoyo,’ musadzakhulupirire. Chifukwa kudzaoneka anthu onama omanena kuti, ‘Ndine Khristu uja,’ kapena kuti, ‘Ndine mneneri.’ Anthuwo azidzachita ntchito zamphamvu ndiponso zinthu zozizwitsa, kuti ngati nkotheka asokeze ngakhale osankhidwa a Mulungu. Koma inu chenjerani. Ine ndiye ndakuuziranitu zonse.” “Masiku amenewo, mavutowo atatha, dzuŵa lidzada, mwezi udzaleka kuŵala. Nyenyezi zidzagwa kuchokera ku thambo, ndipo mphamvu zamumlengalenga zidzagwedezeka. Pamenepo anthu adzaona Mwana wa Munthu akubwera pa mitambo, ali ndi mphamvu zazikulu ndi ulemerero. Tsono Iye adzatuma angelo ake kuti akasonkhanitse osankhidwa ake kuchokera ku mbali zonse, kuyambira ku malekezero ena a dziko lapansi mpaka ku malekezero ake enanso.” “Phunziriraniko kwa mkuyu. Mukamaona kuti nthambi zake zayamba kukhala zanthete ndipo masamba akuphuka, mumadziŵa kuti chilimwe chayandikira. Momwemonso mukadzaona zija ndanenazi zikuchitika, mudzadziŵe kuti Mwana wa Munthu ali pafupi, ali pakhomo penipeni. Ndithu ndikunenetsa kuti zonsezi zidzaoneka anthu a mbadwo unoŵa asanamwalire onse. Thambo ndi dziko lapansi zidzatha, koma mau anga sadzatha mphamvu konse.” “Koma za tsiku lake kapena nthaŵi yake, palibe amene amadziŵa. Angelo omwe akumwamba sadziŵa. Ngakhale Ineyo Mwanane sindidziŵa, amadziŵa ndi Atate okha basi. Tsono chenjerani, khalani maso, chifukwa simudziŵa kuti nthaŵiyo idzakwana liti. Ndi monga ngati bwana amene akunyamuka ulendo kuchoka kunyumba kwake. Amasiya zinthu m'manja mwa antchito ake, aliyense ntchito yake, ndipo amauza wapakhomo kuti azikhala maso. Nanunso tsono khalani maso, chifukwa simudziŵa mwini nyumba adzabwerera nthaŵi yanji: kaya ndi madzulo, kaya ndi pakati pa usiku, kaya ndi tambala woyamba, kapena mbandakucha. Atha kudzabwera mwadzidzidzi, tsono asadzakupezeni muli m'tulo. Zimene ndikunenazi, sindikuuza inu nokha ai, koma ndikuuza anthu onse kuti, ‘Khalani maso.’ ” Kudangotsala masiku aŵiri kuti chifike chikondwerero cha Paska ndi chikondwerero cha masiku odya buledi wosafufumitsa. Akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo ankafunafuna njira yoti amgwirire Yesu mochenjera, nkumupha. Koma ankati, “Zimenezi tisadzachite pa nthaŵi ya chikondwerero ai, pangadzachitike chipolowe pakati pa anthu.” Tsiku lina Yesu anali ku Betaniya, m'nyumba ya Simoni wotchedwa Wakhate. Pamene ankadya, kudafika mai wina atatenga nsupa yagalasi ya mafuta enieni onunkhira, amtengowapatali, a mtundu wa narido. Maiyo adaphwanya nsupa ija, nayamba kuthira mafutawo pamutu pa Yesu. Anthu ena pamenepo adaipidwa nazo nanena kuti, “Chifukwa chiyani kuŵasakaza chotere mafuta onunkhiraŵa? Ndithu mafuta ameneŵa akadatha kuŵagulitsa, pa mtengo wopitirira ndalama zasiliva mazana atatu, kenaka ndalamazo nkukapatsa anthu osauka?” Choncho anthuwo adamupsera mtima mai uja. Koma Yesu adati, “Mlekeni maiyu, mukumuvutiranji kodi? Zimenetu wandichitira iyeyuzi nzabwino kwambiri. Anthu osauka muli nawo nthaŵi zonse, kotero kuti pamene mufuna kuŵachitira zachifundo, mungathe kuŵachitira. Koma Ine simudzakhala nane nthaŵi zonse. Iyeyu wachita zimene akadatha kuchita. Wadzozeratu thupi langa ndi mafuta onunkhira, kuti alikonzeretu lisanaikidwe m'manda. Ndithu ndikunenetsa kuti kulikonse kumene anthu azikalalika Uthenga Wabwino pa dziko lonse lapansi, azidzafotokozanso zimene maiyu wachita, kuti anthu azidzamkumbukira.” Pambuyo pake Yudasi Iskariote, mmodzi mwa ophunzira khumi ndi aŵiri aja, adapita kwa akulu a ansembe kuti akapereke Yesu kwa iwo. Pamene iwo adamva zimenezi adakondwa, ndipo adamlonjeza kuti adzampatsa ndalama. Iyeyo tsono adayamba kufunafuna mpata womuperekera kwa iwo. Pa tsiku loyamba la masiku a buledi wosafufumitsa, tsiku lomwe anthu ankapha mwanawankhosa wochitira phwando la Paska, ophunzira a Yesu adamufunsa kuti, “Kodi tikakukonzereni kuti malo okadyerako phwando la Paska?” Yesu adatuma aŵiri mwa ophunzira ake, naŵauza kuti, “Pitani m'mudzimu. Mukumana ndi munthu wamwamuna atasenza mtsuko wa madzi. Mukamtsatire. Kunyumba kumene ati akaloŵe, mukauze mwini nyumbayo kuti, ‘Aphunzitsi akufunsa kuti, kodi nchiti chipinda cha alendo choti Iwowo adzadyeremo phwando la Paska ndi ophunzira ao?’ Iyeyo akakuwonetsani chipinda chachikulu cham'mwamba, momwe akonzamo zonse zofunikira. M'menemo mukatikonzere chakudya.” Ophunzira aja adanyamuka naloŵa mumzindamo. Adachipezadi monga momwe Yesu adaaŵauzira, ndipo adakonza za phwando la Paska. Kutada, Yesu adabwera ndi ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja. Onse atakhala pansi nkumadya, Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti wina mwa inu, mnzanga wodya nane, andipereka kwa adani anga.” Ophunzirawo adamva chisoni, nayamba mmodzimmodzi kumufunsa kuti, “Monga nkukhala ine?” Yesu adaŵayankha kuti, “Ndi wina ndithu mwa khumi ndi aŵirinu, yemwe akusunsa mkate m'mbalemu pamodzi ndi ine. Mwana wa Munthu akukaphedwadi, monga momwe Malembo akunenera za Iye. Komabe ali ndi tsoka munthu amene akukapereka Mwana wa Munthuyo. Kukadakhala bwino koposa kwa munthu ameneyo, akadapanda kubadwa.” Iwo alikudya choncho, Yesu adatenga mkate, nathokoza Mulungu, nkuunyemanyema, nagaŵira ophunzira aja, ndipo adati, “Kwayani, ili ndi thupi langa.” Kenaka adatenga chikho, nathokoza Mulungu, nkuchipereka kwa ophunzirawo, naamwa onse. Ndipo adaŵauza kuti, “Aŵa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi ameneŵa ndiŵakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka. Kunena zoona, sindidzamwanso chakumwa cha mtengo wamphesachi, mpaka tsiku limene ndidzamwe chatsopano mu Ufumu wa Mulungu.” Tsono ataimba nyimbo yotamanda Mulungu, onse adatuluka nkumapita ku Phiri la Olivi. Pambuyo pake Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Nonsenu mukhumudwa nane nkundisiya. Paja Malembo akuti, ‘Ndidzapha mbusa, ndipo nkhosa zidzangoti balala.’ Koma ndikadzauka kwa akufa, ndidzatsogola ndine kupita ku Galileya.” Petro adati, “Ngakhale onse akhumudwe nkukusiyani, ine ndekha ai.” Yesu adamuuza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti lero lomwe lino usiku womwe uno, tambala asanalire kachiŵiri, ukhala utandikana katatu kuti Ine sundidziŵa.” Apo Petro adanenetsanso kuti, “Ngakhale atati andiphere nanu kumodzi, ine sindingakukaneni konse kuti sindikudziŵani.” Ophunzira ena onse aja nawonso adanena chimodzimodzi. Yesu adapita ndi ophunzira ake aja ku malo ena, otchedwa Getsemani. Tsono adauza ophunzirawo kuti, “Inu bakhalani pano, Ine ndikukapemphera.” Adatengako Petro, Yakobe ndi Yohane. Yesu adayamba kugwidwa ndi chisoni ndi kuvutika mu mtima. Adaŵauza kuti, “Mumtima mwanga muli chisoni chachikulu chofa nacho. Inu khalani pompano, koma mukhale masotu.” Adapita patsogolo pang'ono, nadzigwetsa pansi, nkuyamba kupemphera. Adati, “Ngati nkotheka nthaŵi yoopsa ino indipitirire.” Adanenanso kuti, “Abba, Atate, mungathe kuchita chilichonse. Mundichotsere chikho cha masautsochi. Komabe chitani zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.” Atatero adabwerera kwa ophunzira aja, naŵapeza ali m'tulo. Tsono adafunsa Petro kuti, “Simoni, uli m'tulo kodi iwe? Mongadi walephera kukhala maso ndi kanthaŵi kochepa komwe? Khalani maso inu ndi kumapemphera, kuti mungagwe m'zokuyesani. Mtima ndiye ukufunitsitsadi, koma langokhala lofooka ndi thupi.” Adachokanso nakapemphera ndi mau omwe aja. Pamene adabwerakonso, adaŵapeza ali m'tulo, chifukwa zikope zao zinkalemera ndi tulo. Choncho iwowo adasoŵa choyankha. Pamene adabwerako kachitatu, adati, “Kodi monga mukugonabe ndi kupumula? Basi tsopano. Nthaŵi ija yafika, Mwana wa Munthu akuperekedwa kwa anthu ochimwa. Dzukani, tiyeni tizipita. Suuyu wodzandipereka uja, wafika.” Yesu akulankhula choncho, nthaŵi yomweyo wafika Yudasi, mmodzi mwa ophunzira khumi ndi aŵiri aja. Adaabwera ndi khamu la anthu atatenga malupanga ndi zibonga. Anthuwo adaaŵatuma ndi akulu a ansembe, aphunzitsi a Malamulo ndi akulu a Ayuda. Wodzampereka uja anali ataŵauza chizindikiro kuti, “Yemwe ndikamumpsompsoneyo, ndi ameneyo. Mukamgwire nkupita naye, osamtaya.” Pamene Yudasi adabwera, adadzangofikira pa Yesu, nkunena kuti, “Aphunzitsi!” Atatero adamumpsompsona. Apo anthu aja adamugwira Yesu. Koma wina mwa ophunzira amene anali naye pamenepo, adasolola lupanga lake, natema wantchito wa mkulu wa ansembe onse, mpaka kumusenga khutu. Tsono Yesu adaŵafunsa anthu aja kuti, “Bwanji mwachita kunditengera malupanga ndi zibonga, ngati kuti ndine chigaŵenga? Tsiku ndi tsiku ndidaali nanu m'Nyumba ya Mulungu ndikuphunzitsa, inuyo osandigwira. Koma izi zatere kuti zipherezere zomwe Malembo adanena.” Pamenepo ophunzira ake onse aja adathaŵa, kumsiya yekha. Mnyamata wina ankatsatira Yesu, atangofundira nsalu yokha, opanda chovala china. Anthu aja adaati amgwire, koma iye adaikolopola nsalu ija, nkuthaŵa ali maliseche. Tsono anthu aja adapita naye Yesu kwa mkulu wa ansembe onse. Kumeneko kudaasonkhana onse akulu a ansembe, akulu a Ayuda, ndi aphunzitsi a Malamulo. Petro ankamutsatira Yesu chapatali, mpaka ku bwalo la nyumba ya mkulu wa ansembe uja. Adakhala pansi pamodzi ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu, nkumaotha nao moto. Akulu a ansembe aja ndi onse a m'Bwalo Lalikulu la Ayuda ankafunafuna umboni woneneza Yesu kuti amuphe, koma osaupeza. Ambiritu ankamuneneza zabodza, koma umboni wao sunkagwirizana. Ena adaimirira nayamba kumneneza zabodza. Adati, “Munthu uyu ife tidamumva akunena kuti, ‘Ine ndidzapasula Nyumba ya Mulunguyi, yomangidwa ndi anthu chabe, ndipo patapita masiku atatu ndidzamanga ina yosamangidwa ndi anthu.’ ” Koma ngakhale aponso zokamba zaozo sizinali zogwirizana. Tsono mkulu wa ansembe onse adaimirira pamaso pao, nafunsa Yesu kuti, “Kodi ulibe poyankha? Nzotani zimene anthuŵa akukunenezazi?” Yesu adangokhala chete, osayankha kanthu. Pamenepo mkulu wa ansembe uja adafunsanso kuti, “Kodi ndiwedi Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu Wolemekezeka?” Yesu adayankha kuti, “Inde, ndinedi. Ndipo mudzaona Mwana wa Munthu atakhala ku dzanja lamanja la Mulungu wamphamvuzonse. Mudzamuwona akubwera pa mitambo.” Apo mkulu wa ansembe uja adang'amba zovala zake, nati, “Kodi pamenepa tikusoŵanso mboni zina? Mwadzimvera nokha kunyoza Mulungu koopsaku. Tsono mukuganiza bwanji?” Onse adagamula kuti ayenera kuphedwa. Ena adayamba kumthira malovu, namuphimba m'maso nkumamuwomba makofi, namanena kuti, “Lotatu, wakumenya ndani?” Alonda aja nawonso adayamba kummenya. Petro anali kunsi pa bwalo. Mtsikana wina, wantchito wa mkulu wa ansembe onse, adafika pomwepo. Ataona Petro akuwotha moto, adamuyang'anitsitsa, nati, “Inunsotu munali ndi Yesu wa ku Nazareteyu.” Koma Petro adakana, adati, “Zimenezo ine sindikuzidziŵa, sindikuzimvetsa konse.” Ndipo adatuluka kumapita cha ku chipata. Pamenepo tambala adalira. Koma mtsikana uja adamuwona, nayambanso kuuza amene anali pamenepo kuti, “Akulu ameneŵa anali m'gulu lomweli.” Koma Petro adakananso. Patangopita kanthaŵi, anthu amene adaali pamenepo adamuuza Petro kuti, “Ndithu nawenso ndiwe wa gulu lomweli. Kodi kwanu si ku Galileya iwe?” Koma Petro adayamba kudzitemberera nkumalumbira kuti, “Mtheradi, munthu amene mukunenayu ine sindimdziŵa.” Nthaŵi yomweyo tambala adalira kachiŵiri. Tsono Petro adakumbukira mau aja a Yesu akuti, “Tambala asanalire kaŵiri, ukhala utakana katatu kuti sundidziŵa.” Pomwepo Petro adayamba kulira misozi. M'maŵa kutangocha, akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda ndi aphunzitsi a Malamulo, pamodzi ndi ena onse a m'Bwalo Lalikulu la Ayuda adapanga upo. Adammanga Yesu napita naye kwa Pilato. Pilatoyo adafunsa Yesu kuti, “Kodi iwe, ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Yesu adamuyankha kuti, “Mwanena nokha.” Akulu a ansembe aja adayamba kumneneza zambiri. Pilato adamufunsanso kuti, “Kodi ulibe poyankha? Ona zonse zimene akukunenezazi.” Koma Yesu sadayankhenso kanthu, kotero kuti Pilato adadabwa. Pa nthaŵi ya chikondwerero cha Paska, bwanamkubwa ankaŵamasulira mkaidi mmodzi, yemwe Ayudawo ankapempha. Panali munthu wina, dzina lake Barabasi, amene anali m'ndende pamodzi ndi anthu ena chifukwa choukira Boma ndi kupha anthu. Tsono chikhamu cha anthu chidabwera, nkuyamba kupempha Pilato kuti aŵachitire zomwe adaazoloŵera. Pilato adaŵafunsa kuti, “Kodi mukufuna kuti ndikumasulireni Mfumu ya Ayudayi?” Adaatero chifukwa adaadziŵa kuti Yesuyo akulu a ansembewo angodzampereka chifukwa cha kaduka chabe. Koma akulu a ansembewo adasonkhezera anthu onse aja kuti apemphe kuŵamasulira Barabasi. Tsono Pilato adaŵafunsanso kuti, “Nanga tsono mukuti ndichite naye chiyani uyu amene mukuti ndi Mfumu ya Ayudayu?” Anthuwo adafuula kuti, “Mpachikeni pa mtanda!” Pilato adaŵafunsa kuti, “Adalakwanji?” Koma iwo adafuula koposa kuti, “Mpachikeni pa mtanda!” Choncho Pilato, pofuna kukondwetsa anthuwo, adaŵamasulira Barabasi, nalamula kuti Yesu akwapulidwe. Pambuyo pake adampereka kuti akampachike pa mtanda. Pamenepo asilikali adaloŵetsa Yesu m'bwalo, kunyumba kwa bwanamkubwa, nasonkhanitsa gulu lonse la asilikali anzao. Adamuveka chovala chofiirira, naluka nsangamutu yaminga nkuiika pamutu pake. Kenaka adayamba kumampatsa moni kuti, “Tikuwoneni, mfumu ya Ayuda.” Ankamumenya m'mutu ndi ndodo, namamthira malovu, nkumamugwadira monyodola. Ataseŵera naye mwachipongwe choncho, adamuvula chovala chija, namuvekanso zovala zake. Kenaka adamtenga, nkupita naye kuti akampachike pa mtanda. Pa njira adakumana ndi munthu wina, amene ankadutsa pamenepo kuchokera ku midzi. Munthuyo anali Simoni wa ku Kirene, bambo wake wa Aleksandro ndi Rufu. Tsono asilikali aja adamkakamiza kuti asenze mtanda wa Yesu. Iwowo adapita naye Yesuyo ku malo otchedwa Gologota, (ndiye kuti “Malo a Chibade cha Mutu.”) Adaafuna kumpatsa vinyo wosanganiza ndi mure kuti amwe, koma Iye adakana. Atampachika pa mtanda, adagaŵana zovala zake. Adaachita maere kuti aone zimene aliyense atenge. Pamene adampachika pa mtanda, nkuti nthaŵi ili 9 koloko m'maŵa. Mau osonyeza mlandu womuphera, adaaŵalemba motere, “Mfumu ya Ayuda.” Pamodzi ndi Yesu adaapachikanso pa mitanda zigaŵenga ziŵiri, china ku dzanja lamanja, china ku dzanja lamanzere. [ Motero zidachitikadi zimene mau a Mulungu adaanena kuti, “Adamuyesa mnzao wa anthu ophwanya malamulo.”] Anthu amene ankadutsa pamenepo ankamunyodola. Ankapukusa mitu nkumanena kuti, “Ha, suja iwe unkati, ‘Ndidzapasula Nyumba ya Mulungu nkuimanganso pa masiku atatu?’ Tadzipulumutsatu, tsika pamtandapo!” Nawonso akulu a ansembe ankamuseka, nkumauzana ndi aphunzitsi a Malamulo kuti, “Adapulumutsa anthu ena, koma akulephera kudzipulumutsa Iye yemwe! Uja ankati ndi Mpulumutsi wolonjezedwayu, Mfumu ya Aisraele, atatsikatu tsopano pamtandapa, kuti tiwone ndi kumkhulupirira!” Ndiponso amene adaŵapachika pamodzi naye aja ankamunyoza. Nthaŵi itakwana 12 koloko masana, padaagwa mdima pa dziko lonse mpaka pa 3 koloko. Tsono nthaŵi ili 3 koloko, Yesu adafuula kwakukulu kuti, “Eloi, Eloi, lama sabakatani?” Ndiye kuti, “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?” Atamva mauwo, ena amene adaaimirira pamenepo adati, “Tamverani, akuitana Eliya.” Motero wina adathamanga nakaviika chinkhupule m'vinyo wosasa, nkuchitsomeka ku bango nampatsira, kuti amwe. Anzakewo adati, “Taima, tiwone ngati Eliyayo abweredi kudzamtsitsa.” Koma Yesu adafuula kwakukulu, natsirizika. Chinsalu chochinga chija cha m'Nyumba ya Mulungu chidang'ambika pakatimpakati, kuyambira pamwamba mpaka pansi. Mkulu wa asilikali amene adaaimirira pomwepo kuyang'anana naye, ataona kuti Yesu watsirizika akufuula chotero, adati, “Ndithudi, munthuyu adaalidi Mwana wa Mulungu.” Patali poteropo padaali azimai, akungoyang'anitsitsa. Ena mwa iwo anali Maria wa ku Magadala, ndi Maria, mai wa Yakobe wamng'ono uja ndi wa Yosefe, ndiponso Salome. Azimaiŵa ankatsata Yesu pamene Iye anali ku Galileya, ndi kumamtumikira. Padaalinso azimai ena ambiri omwe adaabwera naye ku Yerusalemuko. Tsopano chisisira chinali chitagwa. Ndiye popeza kuti linali Lachisanu, tsiku lokonzekera Sabata, Yosefe wa ku Arimatea adafika. Adaali mkulu wodziŵika ndithu, wa m'Bwalo Lalikulu la Ayuda. Nayenso ankayembekeza Ufumu wa Mulungu. Tsono iye adalimba mtima, napita kwa Pilato kukapempha kuti ampatsire mtembo wa Yesu. Pilato adaadabwa kumva kuti Yesu wafa kale. Choncho adaitanitsa mkulu wa asilikali uja, namufunsa kuti, “Kodi Yesu wafa kaledi?” Mkulu wa asilikaliyo atavomera, Pilato adamlola Yosefe kuti akatenge mtembowo. Yosefeyo adagula nsalu yoyera yabafuta, natsitsa mtembo uja nkuukuta ndi nsaluyo. Adauika m'manda ochita chosema m'thanthwe, kenaka adagubuduzira chimwala pa khomo kutseka pamandapo. Maria uja wa ku Magadala, ndi Maria mai wa Yosefe, ankaona kumene adamuika Yesu. Tsiku la Sabata ya Ayuda litapita, Maria wa ku Magadala, ndi Maria, mai wa Yakobe, ndiponso Salome adakagula zonunkhira kuti akadzoze mtembo wa Yesu. M'mamaŵa ndithu pa tsiku lotsatira Sabatayo, adapita kumanda kuja, dzuŵa litatuluka. Ankafunsana kuti, “Kodi ndani akatichotsere chimwala cha pakhomo pa manda chija?” Koma poyang'anitsitsa adaona kuti chimwalacho achigubuduza kale; tsonotu chinali chachikuludi. Ataloŵa m'mandamo adaona mnyamata wakhala pansi mbali ya ku dzanja lamanja, atavala mkanjo woyera. Azimaiwo adadzidzimuka. Koma mnyamatayo adaŵauza kuti, “Musade nkhaŵa. Mukufuna Yesu wa ku Nazarete, uja adaampachika pa mtandayu. Wauka, sali muno. Taonani, si apa pamene adaamuika. Koma inu pitani mukauze ophunzira ake, makamaka Petro, kuti, ‘Iye watsogola kunka ku Galileya. Mukamuwonera kumeneko, monga muja adakuuziranimu.’ ” Pamenepo azimaiwo adatuluka nkuthaŵako kumandako, popeza kuti adaagwidwa ndi mantha, mpaka kumangonjenjemera. Ndipo chifukwa cha manthawo sadauze munthu aliyense kanthu. [ Yesu atauka kwa akufa, m'maŵa ndithu, tsiku lotsatira Sabata ya Ayuda, poyambayamba adaaonekera Maria wa ku Magadala, uja adaamtulutsa mizimu yoipa isanu ndi iŵiriyu. Mariayo adapita kukauza amene ankakhala ndi Yesu aja. Iwowo nkuti ali ndi chisoni ndipo akungolira. Ngakhale atamva kuti Yesu ali moyo, ndipo kuti Maria wamuwona, iwo sadakhulupirire. Pambuyo pake Yesu, ali ndi maonekedwe osiyana, adaonekera ophunzira ake ena aŵiri, pamene iwowo anali pa ulendo kunja kwa mzinda wa Yerusalemu. Ophunzirawo adabwerera kudzauza anzao aja, koma iwonso sadaŵakhulupirire. Potsiriza Yesu adaonekera ophunzira khumi ndi mmodzi aja alikudya. Adaŵadzudzula chifukwa cha kusakhulupirira kwao ndi kupulupudza kwao, chifukwa sadakhulupirire anzao aja amene adaamuwona Iye atauka kwa akufa. Tsono adaŵauza kuti, “Pitani ku dziko lonse lapansi, kalalikireni anthu onse Uthenga Wabwino. Amene akakhulupirire ndi kubatizidwa, adzapulumuka, koma amene sakakhulupirira, adzaweruzidwa kuti ngwolakwa. Okhulupirira azidzachita zozizwitsa izi: azidzatulutsa mizimu yoipa potchula dzina langa, azidzalankhula zilankhulo zachilendo, ndipo akagwira njoka kapena kumwa chakumwa chotha kuŵapha, sadzapwetekedwa. Akasanjika manja pa anthu odwala, anthuwo azidzachira.” Ambuye Yesu atalankhula nawo, adatengedwa kupita Kumwamba, nakakhala ku dzanja lamanja la Mulungu. Tsono ophunzira aja adanka nalalika ponseponse. Ambuye ankagwira nawo ntchito pamodzi, ndipo ankatsimikiza mau ao ndi zozizwitsa zimene ankachita.] Ateofilo olemekezeka, Anthu ambiri adayesa kulongosola mbiri ya zinthu zimene zidachitika pakati pathu. Iwo adalemba zimene adaatisimbira anthu oziwona chamaso kuyambira pachiyambi pake, nakhala akuzilalika. Tsono popeza kuti inenso ndalondola mosamala kwambiri m'mene zonsezo zidachitikira kuyambira pa chiyambi, ndaganiza kuti nkwabwino kuti ndikulembereni zimenezo mwatsatanetsatane. Ndatero kuti mudziŵe ndithu kuti zimene adakuphunzitsanizo nzoonadi. Pa nthaŵi imene Herode anali mfumu ya dziko la Yudeya, kunali wansembe wina, dzina lake Zakariya, wa gulu la ansembe la Abiya. Mkazi wake Elizabeti anali wa fuko la Aroni. Aŵiri onsewo anali olungama pamaso pa Mulungu, ndipo ankatsata mokhulupirika malamulo ndi malangizo onse a Ambuye. Adaalibe mwana, chifukwa Elizabeti anali wosabala, ndipo aŵiri onsewo anali okalamba. Tsiku lina Zakariya ankagwira ntchito yake yaunsembe pamaso pa Mulungu. Inali nthaŵi ya gulu lake la ansembe kutumikira. Potsata dongosolo lao la ansembe, iye adaasankhidwa mwamaere kuti akaloŵe m'Nyumba ya Mulungu kukafukiza lubani. Khamu lonse la anthu linkapemphera kunja pa nthaŵi yofukiza lubaniyo. Tsono mngelo wa Ambuye adaonekera Zakariya. Mngeloyo adaaimirira ku dzanja lamanja la guwa lofukizirapo lubani. Zakariya adadzidzimuka pomuwona, nachita mantha. Koma mngeloyo adamuuza kuti, “Usaope, Zakariya, Mulungu wamva pemphero lako. Mkazi wako Elizabeti adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yohane. “Udzakondwa ndi kusangalala, anthu ambirinso adzakondwa chifukwa cha kubadwa kwake, popeza kuti iye adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye. Sazidzamwa konse vinyo kapena choledzeretsa china chilichonse. Adzakhala wodzazidwa ndi Mzimu Woyera ngakhale asanabadwe nkomwe. Adzatembenuza Aisraele ambiri kuti abwerere kwa Ambuye, Mulungu wao. Molimba mtima ndiponso mwamphamvu monga mneneri Eliya, adzatsogolako Ambuye akubwera. Adzayanjanitsanso makolo ndi ana ao, adzatembenuza anthu osamvera kuti akhale ndi nzeru zonga za anthu olungama. Adzakonzera Ambuye anthu okonzekeratu kuŵatumikira.” Zakariya adafunsa mngeloyo kuti, “Kodi ndingadziŵe bwanji kuti zimenezi nzoona? Ineyo ndine nkhalamba, mkazi wanga nayenso wakalamba.” Mngeloyo adati, “Ine ndine Gabriele, amene ndimakhala kufupi ndi Mulungu. Iyeyo wachita kundituma kuti ndilankhule nawe ndi kukuuza uthenga wabwinowu. Iweyo sudakhulupirire zimene ndanenazi, koma zidzachitika ndithu pa nthaŵi yake. Nchifukwa chake udzakhala duu, osatha kulankhula, kufikira tsiku lodzachitika zimenezi.” Nthaŵi yonseyo anthu aja ankadikira Zakariya, nkumadabwa kuti akuchedwa m'Nyumba ya Mulungumo. Pamene iye adatuluka, sadathe kulankhula nawo. Apo iwo adazindikira kuti m'Nyumbamo waona china chake m'masomphenya. Iye adalankhula nawo ndi manja okha, osathanso kunena mau. Atatha masiku ake otumikira m'Nyumba ya Mulungu, adapita kwao. Pambuyo pake mkazi wake Elizabeti adatenga pathupi, nabindikira miyezi isanu. Adati, “Ambuye andichitira zotere: nthaŵi inoyi andiwonetsa chifundo chao, andichotsa manyazi pakati pa anthu.” Elizabeti ali ndi pathupi pa miyezi isanu ndi umodzi, Mulungu adatuma mngelo Gabriele ku mudzi wina wa ku Galileya, dzina lake Nazarete. Adamtuma kwa namwali wina wosadziŵa mwamuna amene anali atafunsidwa mbeta ndi mwamuna, dzina lake Yosefe, wa fuko la mfumu Davide. Namwaliyo dzina lake anali Maria. Mngelo uja adadza kwa iye nati, “Moni, inu amene Mulungu wakukomerani mtima kotheratu. Ambuye ali nanu.” Maria adadzidzimuka nawo kwambiri mau ameneŵa, nayamba kusinkhasinkha kuti kodi moni umenewu ndi wa mtundu wanji? Mngeloyo adamuuza kuti, “Musaope, Maria, Mulungu wakukomerani mtima. Mudzatenga pathupi, ndipo mudzabala mwana wamwamuna. Mudzamutcha dzina lake Yesu. “Adzakhala wamkulu, ndipo adzatchedwa Mwana wa Mulungu Wopambanazonse. Ambuye Mulungu adzamlonga ufumu wa kholo lake Davide, ndipo adzakhala Mfumu ya Aisraele mpaka muyaya. Ufumu wake sudzatha konse.” Koma Maria adafunsa mngeloyo kuti, “Zimenezi zidzachitika bwanji, popeza kuti sindidziŵa mwamuna?” Mngeloyo adayankha kuti, “Mzimu Woyera adzakutsikirani, ndipo mphamvu za Mulungu Wopambanazonse zidzakuphimbani. Nchifukwa chake Mwana wodzabadwayo adzakhala Woyera, ndipo adzatchedwa Mwana wa Mulungu. “Onani, mbale wanu uja Elizabeti, nayenso akuyembekezera mwana wamwamuna mu ukalamba wake. Anthu amati ngwosabala, komabe uno ndi mwezi wake wachisanu ndi chimodzi. Pajatu palibe kanthu kosatheka ndi Mulungu.” Apo Maria adati, “Ndine mtumiki wa Ambuye; zindichitikire monga mwaneneramo.” Ndipo mngeloyo adamsiya. Patapita masiku oŵerengeka, Maria adanyamuka napita mofulumira ku dera lamapiri, ku mudzi wina wa ku Yudeya. Adakaloŵa m'nyumba ya Zakariya, malonjera Elizabeti. Pamene Elizabeti adamva malonje a Maria, mwana adayamba kutakataka m'mimba mwake. Elizabeti adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo adalankhula mokweza mau kuti, “Ndinu odala kupambana akazi ena onse, ngwodalanso Mwana wanu. Ine ndine yani kuti inu, mai wa Ambuye anga, mudzandiyendere? Chifukwatu pamene ndinamva malonje anu, mwana anayamba kutakataka ndi chimwemwe m'mimba mwanga. Ndinu odala chifukwa mudakhulupirira kuti zimene Ambuye adakuuzani, zidzachitadi.” Pamenepo Maria adati, “Mtima wanga ukutamanda Ambuye, ndipo mzimu wanga ukukondwera mwa Mulungu, Mpulumutsi wanga, popeza kuti wayang'ana kutsika kwa mtumiki wake. Ndithu kuyambira tsopano anthu a mibadwo yonse adzanditcha wodala, pakuti Iye amene ali wamphamvu wandichitira zazikulu, ndipo dzina lake nloyera. Amaŵachitira chifundo anthu a mibadwo ndi mibadwo amene amamlemekeza. Wachita zamphamvu ndi dzanja lake, wabalalitsa anthu a mtima wonyada. Mafumu amphamvu waŵatsitsa pa mipando yao yachifumu, anthu wamba nkuŵakweza. Anthu anjala waŵakhutitsa ndi zabwino, anthu olemera nkuŵabweza osaŵapatsa kanthu. Wadzathandiza anthu ake Aisraele, pokumbukira chifundo chake. Izi ndi zomwe adaalonjeza kuti adzaŵachitira makolo athu akale aja, Abrahamu ndi zidzukulu zake mpaka muyaya.” Maria atakhala ndi Elizabeti ngati miyezi itatu, adabwerera kwao. Nthaŵi yakuti Elizabeti achire idakwana, ndipo adabala mwana wamwamuna. Anzake ndi abale ake atamva kuti Ambuye amchitira chifundo chachikulu chotere, adakondwera naye pamodzi. Pa tsiku lachisanu ndi chitatu mwanayo atabadwa, adadza naye kuti amuumbale, nafuna kumutcha dzina la bambo wake Zakariya. Koma mai wake adakana, adati, “Iyai, koma atchedwe Yohane.” Pamenepo anthuwo adamuuza kuti, “Koma pakati pa abale anu palibe amene ali ndi dzina limeneli.” Tsono adalankhula ndi bambo wake ndi manja, namufunsa kuti, “Mukufuna kuti timutche dzina lanji?” Zakariya adapempha cholemberapo, nalembapo kuti, “Dzina lake ndi Yohane.” Anthu onsewo adazizwa. Pomwepo Zakariya adathanso kulankhula, nayamba kutamanda Mulungu. Anzao onse aja adagwidwa ndi mantha, ndipo mbiri ya zimenezi idawanda ku dera lonse la mapiri a ku Yudeya. Anthu onse amene ankazimva, ankazilingalira m'mitima mwao, ndi kumadzifunsa kuti, “Kodi mwana ameneyu adzakhala munthu wotani?” Pakuti zinkachita kuwonekeratu kuti Ambuye anali naye. Tsono Zakariya, bambo wa Yohaneyo, adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula mau ochokera kwa Mulungu. Adati, “Atamandike Ambuye, Mulungu wa Aisraele, chifukwa adadzayendera anthu ao, ndi kudzaŵaombola. Adautsa wina, wa fuko la mtumiki wake Davide, kuti akhale Mpulumutsi wathu wamphamvu. Izi ndi zomwe Iye adaaneneratu kalekale kudzera mwa aneneri ake oyera mtima. Adaalonjeza kuti adzatipulumutsa kwa adani athu, ndi kwa onse odana nafe. Choncho Iye waŵachitiradi chifundo makolo athu akale, ndipo wakumbukira chipangano chake choyera. Adalonjezanso Abrahamu, kholo lathu, molumbira, kuti adzatipulumutsa kwa adani athu, kuti tizimtumikira mopanda mantha, kuti tikhale oyera mtima ndi olungama pamaso pake, masiku onse a moyo wathu. Tsono mwana iwe, udzatchedwa mneneri wa Mulungu Wopambanazonse, chifukwa udzatsogola pamaso pa Ambuye, kuti ukonzeretu njira zao. Udzadziŵitsa anthu ao kuti Mulungu adzaŵapulumutsa pakuŵakhululukira machimo ao. Mulungu wathu ndi wa chifundo chachikulu, adzatitumizira kuŵala kwa dzuŵa lam'maŵa kuchokera Kumwamba. Kuŵala kwake kudzaunikira onse okhala mu mdima wabii ngati wa imfa, kudzatitsogolera pa njira ya mtendere.” Mwana uja Yohane ankakula nasanduka wa mkhalidwe wamphamvu. Pambuyo pake adakhala ku chipululu mpaka tsiku limene adadziwonetsa poyera pakati pa Aisraele. Masiku amenewo, Augusto, Mfumu ya ku Roma, adalamula kuti pakhale kalembera wa anthu a m'maiko ake onse. Kalembera ameneyu anali woyamba, ndipo adachitika pamene Kwirinio anali bwanamkubwa wa dziko la Siriya. Motero anthu onse adapita kukalembedwa, aliyense ku mudzi kwao. Yosefe nayenso adanyamuka kuchokera ku Nazarete, mudzi wa ku Galileya. Adapita ku Yudeya, ku mudzi wa mfumu Davide, dzina lake Betelehemu, chifukwa anali wa m'banja ndi fuko la Davideyo. Adapita kukalembedwa pamodzi ndi Maria, mkazi wake, amene anali ndi pathupi. Pamene anali kumeneko, nthaŵi yake yoti Maria achire idakwana, ndipo adabala mwana wake wachisamba wamwamuna. Adamkulunga m'nsalu namgoneka m'chodyera cha zoŵeta, chifukwa adaasoŵa malo m'nyumba ya alendo. Ku dera lomwelo kunali abusa amene ankalonda zoŵeta zao ku dambo usiku. Mwadzidzidzi mngelo wa Ambuye adadzaimirira pakati pao, ndipo ulemerero wa Ambuye udaŵala ponse pozungulira, mwakuti abusawo adaachita mantha kwambiri. Koma mngeloyo adaŵauza kuti, “Musaope, ndadzakuuzani uthenga wabwino, umene udzakondweretsa anthu onse kwambiri. Usiku womwe uno m'mudzi wa Davide wakubadwirani Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye. Chitsimikizo chake ndi ichi: mukapeza mwana wakhanda, wokutidwa ndi nsalu, atagona m'chodyera cha zoŵeta.” Mwadzidzidzi pamodzi ndi mngeloyo padaoneka gulu lalikulu la angelo ena. Ankatamanda Mulungu ndi mau akuti, “Ulemerero kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndipo pansi pano mtendere pakati pa anthu amene Iye amakondwera nawo.” Angelowo atachoka kubwerera Kumwamba, abusa aja adayamba kuuzana kuti, “Tiyeni tipite ku Betelehemu, tikaone zachitikazi, zimene Ambuye atidziŵitsa.” Tsono adapita mofulumira, nakapeza Maria ndi Yosefe, atagoneka mwana wakhandayo m'chodyera cha zoŵeta chija. Pamene adamuwona, abusawo adaŵafotokozera zimene mngelo uja adaaŵauza za mwanayo. Onse amene ankamva, ankadabwa ndi zimene abusawo ankaŵasimbira. Koma Maria adasunga zonsezo namazilingalira mumtima mwake. Pambuyo pake abusa aja adabwerera akuyamika ndi kutamanda Mulungu chifukwa cha zonse zimene anali atamva ndi kuziwona. Zonse zinali monga momwe mngelo uja adaaŵauzira. Patapita masiku asanu ndi atatu, mwana uja adamuumbala namutcha dzina lake Yesu. Dzinali ndi lomwe lija limene mngelo adaatchula, Maria asanatenge pathupi. Kenaka idafika nthaŵi yoti Yosefe ndi Maria achite mwambo wakuyeretsedwa potsata Malamulo a Mose. Tsono mwanayo adapita naye ku Yerusalemu kuti akampereke kwa Ambuye. Pajatu m'Malamulo a Ambuye muli mau akuti, “Mwana aliyense wamwamuna, woyamba kubadwa, apatulidwe kuti akhale wao wa Ambuye.” Adakaperekanso nsembe potsata Malamulo a Ambuye akuti, “Apereke njiŵa ziŵiri kapena maunda aŵiri.” Ku Yerusalemuko kunali munthu wina, dzina lake Simeoni. Anali munthu wolungama ndi woopa Mulungu. Ankayembekezera nthaŵi yoti Mulungu adzapulumutse Aisraele, ndipo Mzimu Woyera anali naye. Mzimu Woyerayo adaamuululira kuti sadzafa asanaone Mpulumutsi amene Mulungu adaalonjeza. Tsiku lina Mzimu Woyera adamlamula kuti apite ku Nyumba ya Mulungu. Makolo a Yesu adaloŵanso m'Nyumbamo ndi mwana waoyo kukamchitira mwambo potsata Malamulo a Mose. Pamenepo Simeoni adalandira mwanayo m'manja mwake, nayamba kutamanda Mulungu ndi mau akuti, “Ambuye, tsopano mundilole ine mtumiki wanu, ndipite ndi mtendere, pakuti mwachitadi zija mudaalonjezazi. Ndi maso angaŵa ndachiwonadi chipulumutso chija, chimene mudakonza kuti anthu a mitundu yonse achiwone. Mwapereka kuŵala kodzaunikira anthu a mitundu ina, kodzakhala ulemerero wa anthu anu Aisraele.” Atate ndi amai a mwanayo ankangodabwa nazo zimene Simeoni ankanena za mwanayo. Kenaka Simeoniyo adaŵadalitsa, nauza Maria, mai wa mwanayo, kuti, “Mwanayu Mulungu wamuika kuti Aisraele ambiri adzagwe, ambirinso adzadzuke, chifukwa cha iyeyu. Adzakhala chizindikiro chochokera kwa Mulungu, chimene anthu ambiri adzatsutsana nacho, kuti choncho maganizo amene ali m'mitima ya anthu ambiri adzaonekere poyera. Ndipo inunso mai, chisoni chidzabaya mtima wanu ngati lupanga.” Kunalinso mneneri wina wamkazi, dzina lake Anna, mwana wa Fanuwele, wa fuko la Asere. Anali wokalamba kwambiri. Anali atakhala pa banja zaka zisanu ndi ziŵiri zokha, pambuyo pake nkukhala wamasiye kufikira msinkhu wa zaka 84. Sankachokatu ku Nyumba ya Mulungu, ankakonda kudzatumikira Mulungu usana ndi usiku pakupemphera ndi kusala zakudya. Iye adafikako nthaŵi yomweyo, nayamba kuyamika Mulungu, nkumakamba za Mwanayo ndi anthu onse amene ankayembekezera nthaŵi yoti Mulungu adzapulumutse Yerusalemu. Yosefe ndi Maria atachita zonse potsata Malamulo a Ambuye, adabwerera ku Galileya, kumudzi kwao ku Nazarete. Mwanayo ankakula, nasanduka wamphamvu nkukhalanso wa nzeru zabasi. Ndipo Mulungu ankamudalitsa. Makolo a Yesu ankapita ku Yerusalemu chaka ndi chaka ku chikondwerero cha Paska. Pamene Yesu anali ndi zaka khumi ndi ziŵiri, iwo adapita kumeneko monga adaazoloŵera. Masiku a chikondwererocho atatha, adanyamuka kumabwerera kwao, mnyamata uja Yesu nkutsalira ku Yerusalemu, makolo ake osadziŵa. Iwo ankayesa kuti ali pamodzi ndi anzao aulendo, choncho adayenda ulendo wa tsiku limodzi. Tsono adayamba kumufunafuna pakati pa abale ao ndi abwenzi ao. Ataona kuti sakumpeza, adabwerera ku Yerusalemu akumufunafuna ndithu. Patapita masiku atatu, adampeza m'Nyumba ya Mulungu, atakhala pakati pa aphunzitsi, akumvetsera mau ao, ndi kumaŵafunsa mafunso. Onse amene ankamva mau ake, ankadabwa ndi mayankho ake anzeru. Pamene makolo ake adamuwona, adadabwa, ndipo mai wake adamufunsa kuti, “Mwana iwe, watisautsiranji chotere? Ine ndi bambo wako tavutika nkukufunafuna.” Koma Yesu adati, “Mumandifunafuna chifukwa chiyani? Kani simumadziŵa kuti ndiyenera kupezeka m'nyumba ya Atate anga?” Koma iwo sadamvetse zimene adaŵayankhazo. Tsono Yesu adabwerera nawo pamodzi, nafika ku Nazarete, ndipo ankaŵamvera. Mai wake ankasunga zonsezi mumtima mwake. Ndipo Yesu analikunka nakula m'nzeru ndi mu msinkhu, ndipo Mulungu ndi anthu omwe ankakondwera naye kwambiri. Pa chaka cha khumi ndi chisanu cha ufumu wa Tiberio, mfumu ya ku Roma, Ponsio Pilato anali bwanamkubwa ku Yudeya. Herode ankalamulira ku dera la Galileya. Filipo, mbale wake, ankalamulira ku dera la Itureya ndi ku dera la Trakoniti. Lisaniasi ankalamulira ku dera la Abilene, ndipo Anasi ndi Kayafa anali akulu a ansembe onse. Pa nthaŵi imeneyo Mulungu adampatsira uthenga Yohane uja, mwana wa Zakariya, m'chipululu. Choncho Yohaneyo adayendera dziko lonse lozungulira mtsinje wa Yordani, akulalika. Ankauza anthu kuti, “Tembenukani mtima ndi kubatizidwa, kuti Mulungu akukhululukireni machimo anu.” Izi zidachitika monga zidaalembedwera m'buku la mneneri Yesaya kuti, “Liwu la munthu wofuula m'chipululu: akunena kuti, ‘Konzani mseu wodzadzeramo Ambuye, ongolani njira zoti adzapitemo. Dzazani chigwa chilichonse, chepetsani phiri lililonse ndi mtunda uliwonse. Ongolani njira zokhotakhota, salazani njira zazigolowondo. Motero anthu onse adzaona chipulumutso chochokera kwa Mulungu.’ ” Anthu ambirimbiri ankabwera kuti iye aŵabatize. Tsono iyeyo ankati, “Ana a njoka inu, adakuchenjezani ndani kuti muthaŵe chilango cha Mulungu chikudzachi? Chitanitu ntchito zosonyeza kuti mwatembenukadi mtima. Ndipo m'mitima mwanu musayambe zomanena kuti, ‘Atate athu ndi Abrahamu.’ Ndithu ndikunenetsa kuti Mulungu angathe kusandutsa ngakhale miyala ili apayi kuti ikhale ana a Abrahamu. Pali pano nkhwangwa ili kale patsinde pa mitengo. Choncho mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino, adzaudula nkuuponya pa moto.” Pamenepo anthu aja adafunsa Yohane kuti, “Tsono ife tizichita zabwino zanji?” Iye adati, “Amene ali ndi miinjiro iŵiri, apatseko mnzake amene alibe. Ndipo amene ali nacho chakudya, achitenso chimodzimodzi.” Kudabweranso okhometsa msonkho kuti Yohane aŵabatize. Iwo adamufunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi ife tizichita zabwino zanji?” Iye adati, “Musamakhometsa msonkho moonjezera pa zimene adakulamulani.” Asilikali omwe adamufunsa kuti, “Nanga ifeyo tizichita zabwino zanji?” Iye adati, “Musamalanda za munthu aliyense pakuwopseza kapena pakumnamizira. Muzikhutira ndi malipiro anu.” Chiyembekezo cha anthu chidayamba kukula, ndipo onse ankaganiza za Yohane kuti kapena ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja. Tsono Yohane ankaŵauza onse kuti, “Ine ndimakubatizani ndi madzi, koma akubwera wina woposa ine. Ameneyo ine ndine wosayenera ngakhale kumasula zingwe za nsapato zake. Iyeyo adzakubatizani mwa Mzimu Woyera ndiponso m'moto. Chopetera chake chili m'manja kuti apete tirigu wake. Tsono adzathira tirigu m'nkhokwe, koma mankhusu adzaŵatentha m'moto wosazimika.” Yohane ankalalikira anthu Uthenga Wabwino pakuŵalangiza motero, ndiponso mwa njira zina zambiri. Komanso adadzudzula mfumu Herode chifukwa chokwatira Herodiasi, mkazi wa mbale wake, ndiponso chifukwa cha zoipa zina zambiri zimene ankachita. Pambuyo pake, kuwonjezera pa zonsezi, Herode adatsekera Yohaneyo m'ndende. Tsiku lina anthu onse aja atabatizidwa, Yesu nayenso adabatizidwa. Pamene Iye ankapemphera, kuthambo kudatsekuka, ndipo Mzimu Woyera adatsikira pa Iye, akuwoneka ndi thupi ngati la nkhunda. Tsono kudamveka mau ochokera Kumwamba akuti, “Iwe ndiwe Mwana wanga wapamtima. Ndimakondwera nawe kwambiri.” Yesu anali ndi zaka ngati makumi atatu pamene adayamba ntchito yake ya kuphunzitsa. Anthu ankamuyesa mwana wa Yosefe, amene anali mwana wa Eli, mwana wa Matati, mwana wa Levi, mwana wa Meliki, mwana wa Yanai, mwana wa Yosefe, mwana wa Matatiasi, mwana wa Amosi, mwana wa Nahumu, mwana wa Hesili, mwana wa Nagai, mwana wa Mahati, mwana wa Matatiasi, mwana wa Semeini, mwana wa Yoseke, mwana wa Yoda, mwana wa Yohanani, mwana wa Resa, mwana wa Zerubabele, mwana wa Salatiele, mwana wa Neri, mwana wa Meliki, mwana wa Adi, mwana wa Kosamu, mwana wa Elimadama, mwana wa Ere, mwana wa Yose, mwana wa Eliezere, mwana wa Yorimu, mwana wa Matati, mwana wa Levi, mwana wa Simeoni, mwana wa Yudasi, mwana wa Yosefe, mwana wa Yonamu, mwana wa Eliyakimu, mwana wa Melea, mwana wa Mena, mwana wa Matata, mwana wa Natamu, mwana wa Davide, mwana wa Yese, mwana wa Obede, mwana wa Bowazi, mwana wa Sala, mwana wa Nasoni, mwana wa Aminadabu, mwana wa Adimini, mwana wa Arini, mwana wa Hesiromu, mwana wa Perezi, mwana wa Yuda, mwana wa Yakobe, mwana wa Isaki, mwana wa Abrahamu, mwana wa Tera, mwana wa Nahoro, mwana wa Serugi, mwana wa Reu, mwana wa Pelegi, mwana wa Ebere, mwana wa Sela, mwana wa Kainani, mwana wa Arifaksadi, mwana wa Semu, mwana wa Nowa, mwana wa Lameki, mwana wa Metusela, mwana wa Enoki, mwana wa Yaredi, mwana wa Mahalalele, mwana wa Kainani, mwana wa Enosi, mwana wa Seti, mwana wa Adamu, amene anali mwana wa Mulungu. Yesu, ali wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, adabwerako ku mtsinje wa Yordani kuja. Mzimu Woyerayo ankamutsogolera m'chipululu masiku makumi anai, ndipo kumeneko Satana ankamuyesa. Yesu sankadya kanthu masiku amenewo, ndipo pamene masikuwo adatha, adamva njala. Tsono Satana adamuuza kuti, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, lamulani mwala uli apawu kuti usanduke chakudya.” Koma Yesu adati, “Malembo akuti, ‘Munthu sangakhale moyo ndi chakudya chokha.’ ” Pambuyo pake Satana adatenga Yesu kupita naye pa malo okwera, ndipo pa kamphindi kakang'ono adamuwonetsa maiko a mafumu onse a pansi pano. Tsono adamuuza kuti, “Ndidzakupatsani ulamuliro ndi ulemerero wonsewu, chifukwa zidapatsidwa kwa ine, ndipo ndimazipatsa aliyense amene ndifuna. Choncho mukandipembedza, zonsezi zidzakhala zanu.” Apo Yesu adati, “Malembo akuti, ‘Uzipembedza Ambuye Mulungu wako, ndipo uziŵatumikira Iwo okha.’ ” Potsiriza Satana adatenga Yesu kupita naye ku Yerusalemu, nakamuimika pamwamba penipeni pa Nyumba ya Mulungu. Adamuuza kuti, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, mudziponye pansi. Paja Malembo akuti, “ ‘Mulungu adzalamula angelo ake kuti akusamaleni.’ Ndiponso, “ ‘Iwo adzakunyamulani m'manja mwao, kuti mapazi anu angapweteke pa miyala.’ ” Koma Yesu adati, “Malembo akuti, ‘Usaŵayese Ambuye, Mulungu wako.’ ” Tsono Satana atatha kumuyesa mwa zonsezi, adalekana naye, kudikira nthaŵi ina. Yesu adabwereranso ku Galileya ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Mbiri yake idawanda kuzungulira dziko lonselo. Ankaphunzitsa m'nyumba zao zamapemphero, ndipo anthu onse ankamutamanda. Nthaŵi ina Yesu adafika ku Nazarete kumene adaaleredwa. Ndipo pa tsiku la Sabata adaloŵa m'nyumba yamapemphero, monga adaazoloŵera, naimirira kuti aŵerenge mau. Adampatsa buku la mneneri Yesaya. Tsono Iye adafutukula bukulo, napeza pamene padalembedwa kuti, “Mzimu wa Chauta wadzaza mwa Ine. Wandidzoza kuti ndikalalikire amphaŵi Uthenga Wabwino. Wandituma kuti ndikalengeze kwa am'ndende kuti adzamasulidwa, ndi kwa akhungu kuti adzapenyanso. Wandituma kuti ndikaŵapatse ufulu anthu osautsidwa, ndi kukalalika za nthaŵi imene Ambuye adzapulumutsa anthu ao.” Yesu adatseka bukulo nkulipereka kwa mtumiki wa nyumba yamapemphero, nakhala pansi. Anthu onse amene adaasonkhana m'nyumbamo ankangomupenyetsetsa. Tsono Yesu adaŵauza kuti, “Lero zachitikadi zimene adaaneneratu Malembo amene mwamvaŵa.” Anthu onse adamtamanda, nkumadabwa ndi mau ogwira mtima amene Iye ankalankhula. Anthuwo ankati, “Kodi uyu si mwana uja wa Yosefeyu?” Apo Yesu adaŵauza kuti, “Ndithudi mudzandiwuza mwambi uja wakuti, ‘Iwe sing'anga, dzichiritse wekha.’ Mudzatinso, ‘Tidamva zimene mudachita ku Kapernao, tsono muchitenso zomwezo kwanu kuno.’ ” Adaŵauzanso kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti palibe mneneri amene amalandiridwa bwino kumudzi kwao. Kunena zoona, paja panali azimai amasiye ambiri pakati pa Aisraele pa nthaŵi ya mneneri Eliya, pamene mvula siidagwe zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi, kotero kuti munali njala yaikulu m'dziko lonse. Eliya sadatumidwe ndi kwa mmodzi yemwetu mwa iwo aja, koma adatumidwa kwa mai wamasiye wa ku mudzi wa Sarepta, m'dziko la Sidoni. Panalinso akhate ambiri pakati pa Aisraele nthaŵi ya mneneri Elisa, komabe panalibe ndi mmodzi yemwe mwa iwo aja amene adachiritsidwa. Amene adachiritsidwa ndi Namani yekha wa ku dziko la Siriya.” Anthu onse amene anali m'nyumba yamapemphero muja atamva mau ameneŵa, adapsa mtima kwambiri. Adaimirira namtulutsira kunja kwa mudzi, nkupita naye pamwamba pa phiri pamene adaamangapo mudzi wao. Adaati akamponye kunsi, koma Iye adangodzadutsa pakati pao, nkumapita. Yesu adapita ku Kapernao, mudzi wina wa ku Galileya, nkumaphunzitsa pa tsiku la Sabata. Zophunzitsa zake anthu zidaaŵagwira mtima kwambiri, chifukwa ankalankhula moonetsa ulamuliro ngati mwiniwake. M'nyumba yamapempheroyo munali munthu wogwidwa ndi mzimu womuipitsa. Adalankhula mokuwa kuti, “Aah, kodi takuputani chiyani, Inu Yesu wa ku Nazarete? Kodi mwadzatiwononga? Ndakudziŵani, ndinu Woyera uja wa Mulungu.” Koma Yesu adazazira mzimu woipawo, adati, “Khala chete, tuluka mwa munthuyu.” Apo mzimu womuipitsa uja udamugwetsa pansi munthuyo pakati pa anthu, nkutuluka, osamupweteka konse. Anthu onse aja adazizwa, mpaka kumafunsana kuti, “Mau ameneŵa ngotani? Ngakhale mizimu yoipitsa anthu yomwe akuilamula ndi mphamvu ndi ulamuliro, ndipo ikutulukadi.” Motero mbiri ya Yesu idawanda ku dera lonselo. Yesu adanyamuka nachoka ku nyumba yamapemphero kuja, nakaloŵa m'nyumba ya Simoni. Apongozi a Simoni ankadwala malungo aakulu, ndipo anthu adapempha Yesu kuti achitepo kanthu. Yesu adaŵeramira pa iye, nazazira malungowo, ndipo malungo aja adatha. Pomwepo amai aja adadzuka nayamba kukonzera anthu chakudya. Dzuŵa likuloŵa, anthu onse amene anali ndi anzao odwala nthenda zosiyanasiyana, adabwera nawo kwa Yesu. Iye adasanjika manja pa wodwala aliyense, naŵachiritsa onse. Nayonso mizimu yoipa inkatuluka mwa anthu ambiri ikufuula nkumanena kuti, “Inu ndinu Mwana wa Mulungu.” Koma Iye adaidzudzula, osailola kuti ilankhule, chifukwa idaadziŵa kuti analidi Mpulumutsi wolonjezedwa uja. Kutacha, Yesu adachoka ku Kapernao kuja napita ku malo kosapitapita anthu. Makamu a anthu adayamba kumufunafuna, ndipo atampeza, adayesa kumletsa kuti asaŵasiye. Koma Iye adaŵauza kuti, “Ndiyenera kukalalika Uthenga Wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu ku midzi inanso, pakuti ndizo zimene Mulungu adanditumira.” Motero Iye ankalalika m'nyumba zamapemphero za ku Yudeya. Tsiku lina Yesu adaaimirira pamphepete pa nyanja ya Genesarete, anthu ambirimbiri nkumamupanikiza kuti amve mau a Mulungu. Iye adaona zombo ziŵiri pamphepetepo. Asodzi anali atatulukamo, ndipo ankatsuka makoka ao. Yesu adaloŵa m'chombo chimodzi, chimene chinali cha Simoni, nampempha kuti asunthire pang'ono ku nyanja. Adakhala pansi, ndipo ali m'chombo momwemo, adayamba kuŵaphunzitsa anthuwo. Atatsiriza kulankhula, adauza Simoni kuti, “Sunthirani kozamako, muponye makoka anu kuti muphe nsomba.” Simoni adati, “Aphunzitsi, usiku wonsewu takhalira kugwira ntchito, osapha kanthu, koma chifukwa Inuyo mwatero, chabwino ndiponya makoka.” Tsono iwo adaponyadi makoka, napha nsomba zambirimbiri, kotero kuti makokawo ankayamba kung'ambika. Adachita kukodola anzao a m'chombo china chija kuti adzaŵathandize. Iwo adabwera, ndipo adadzaza zombo ziŵiri zonse zija mpaka zinali pafupi kumira. Pamene Simoni Petro adaona zimenezo, adagwada nkuŵerama kwambiri pamaso pa Yesu nati, “Pepani Ambuye, mundichokere, ndine munthu wochimwa.” Adaatero popeza kuti iye, pamodzi ndi onse amene anali naye, adaazizwa nako kuchuluka kwa nsomba zimene adaaphazo. Yakobe ndi Yohane, ana a Zebedeo, anzake a Simoni, nawonso adaazizwa. Tsono Yesu adauza Simoni kuti, “Usaope, kuyambira tsopano udzakhala msodzi wa anthu.” Motero, atakokera zombozo ku mtunda, adasiya zonse namatsata Yesu. Pamene Yesu anali m'mudzi wina, kudabwera munthu wina wa khate thupi lonse. Pamene adaona Yesu, adadzigwetsa moŵerama pansi pamaso pake nayamba kumdandaulira. Adati, “Ambuye, mutafuna, mungathe kundichiritsa.” Yesu adatambalitsa dzanja nkumukhudza, nati, “Chabwino, ndikufuna, chira!” Pomwepo khate lake lija lidatha. Tsono Yesu adamuuza kuti, “Chenjera, usakambire wina aliyense zimenezi. Ingopita, ukadziwonetse kwa wansembe ndipo ukapereke nsembe adalamula Mose ija. Imeneyo ikhale yotsimikizira anthu onse kuti wachiradi.” Komabe mbiri ya Yesu inkawandirawandira, ndipo makamu ambiri a anthu ankasonkhana kuti amve mau ake, ndiponso kuti aŵachize nthenda zao. Koma Iye adapita kumalo kosapitapita anthu, namakapemphera kumeneko. Tsiku lina Yesu ankaphunzitsa. Pomwepo padaakhala Afarisi ena ndi aphunzitsi ena a Malamulo, ochokera ku midzi yonse ya ku Galileya, ndi ya ku Yudeya, ndiponso ku Yerusalemu. Mphamvu zochokera kwa Ambuye zinali mwa Iye kuti azichizira odwala. Tsono kudafika anthu ena ndi munthu wofa ziwalo, atamnyamulira pa machira. Adayesa kuloŵa naye m'nyumba kuti amkhazike pamaso pa Yesu. Koma chifukwa anthu adaachuluka, sadapeze poloŵera naye. Motero adakwera pa denga, nachotsapo mapale ena, nkumutsitsa ndi machira ake omwe kumufikitsa pansi pakati pa anthu, pamaso pa Yesu. Poona chikhulupiriro chaocho, Yesu adati, “Mbale wanga, machimo ako akhululukidwa.” Apo aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi aja adayamba kudzifunsa mumtima mwao kuti, “Ndaninso kodi amene akunyoza Mulungu mwachipongweyu? Ndani angakhululukire machimo, si Mulungu yekha kodi?” Yesu adaadziŵa maganizo ao, ndiye adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukuganiza zimenezo mumtima mwanu? Chapafupi koposa nchiti, kunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kunena kuti, ‘Dzuka, yamba kuyenda?’ Koma kuti mudziŵe kuti Mwana wa Munthu ali nazo mphamvu pansi pano zokhululukira machimo, onani.” Pamenepo adauza wofa ziwalo uja kuti, “Iwe, ndikuti dzuka, tenga machira ako, uzipita kumudzi.” Pomwepo wodwalayo adadzukadi onse akupenya, ndipo adatenga machira aja amene adaagonapo, namapita kwao akutamanda Mulungu. Anthu onse aja adazizwa kwambiri, nayamba kutamanda Mulungu. Adagwidwa ndi mantha nati, “Taona zodabwitsa lero.” Pambuyo pake Yesu adatuluka naona munthu wokhometsa msonkho, dzina lake Levi, ali pa ntchito m'nyumba ya msonkho. Adamuuza kuti, “Iwe, unditsate.” Iye adanyamuka, nasiya zonse, nkumamutsatadi. Tsono Levi adamkonzera Yesu phwando lalikulu kunyumba kwake. Okhometsa msonkho ambirimbiri, pamodzi ndi anthu ena, anali nao paphwandopo. Afarisi pamodzi ndi aphunzitsi ao a Malamulo adayamba kuŵinya, nafunsa ophunzira ake kuti, “Bwanji mukudya ndi kumwa pamodzi ndi okhometsa msonkho, ndi anthu ochimwa?” Yesu adaŵayankha kuti, “Anthu amene ali bwino sasoŵa sing'anga ai, koma amene akudwala. Inetu sindidabwere kudzaitana anthu olungama, koma anthu ochimwa, kuti atembenuke mtima.” Anthu ena adauza Yesu kuti, “Ophunzira a Yohane amasala zakudya kaŵirikaŵiri nkumapemphera, chimodzimodzinso ophunzira a Afarisi. Koma ophunzira anu amangodya ndi kumwa.” Yesu adati, “Kani anzake a mkwati angathe kumasala zakudya pamene mkwati ali nao pomwepo? Chosatheka! Koma idzafika nthaŵi pamene adzaŵachotsera mkwatiyo. Pamenepo ndiye azidzasala zakudya.” Yesu adaŵapheranso fanizo, adati, “Munthu sang'amba chigamba ku chovala chatsopano nkuchisokerera pa chovala chakale. Chifukwa akatero, waononga chovala chatsopanocho, ndipo chigamba chatsopanocho sichidzayenerana ndi chovala chakale chija. “Ndiponso munthu sathira vinyo watsopano m'matumba achikopa akale. Chifukwa akatero, vinyo watsopanoyo amaphulitsa matumba aja. Choncho vinyoyo adzatayika, matumbawo nkutha ntchito. Koma vinyo watsopano amamuthira m'matumba atsopanonso. “Ndipo munthu akangolaŵa vinyo wakale, watsopano sangamufune. Pajatu amati, ‘Wakale ndiye vinyo chaiye.’ ” Pa tsiku lina la Sabata Yesu ankadutsa m'minda ya tirigu. Ophunzira ake ankathyolako ngala za tirigu, namazifikisa ndi manja, nkumadya. Apo Afarisi ena adafunsa kuti, “Bwanji mukuchita zimene siziloledwa pa tsiku la Sabata?” Yesu adati, “Kani simudaŵerenge zimene adaachita Davide, pamene iye ndi anzake adaazingwa nayo njala? Suja adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, natenga buledi woperekedwa kwa Mulungu, naadya, nkupatsakonso anzake aja? Chonsecho nkosaloledwa kuti buledi ameneyo wina aliyense nkumudya kupatula ansembe okha.” Tsono Yesu popitiriza adaŵauza kuti, “Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro wonse pa zokhudza tsiku la Sabata.” Pa tsiku lina la Sabata Yesu adaloŵa m'nyumba yamapemphero nkumaphunzitsa. M'menemo munali munthu wina wopuwala dzanja lamanja. Aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi ankafuna chifukwa choti akamnenezere Yesuyo, motero ankamuyang'anitsitsa kuti aone ngati achiritse munthu pa tsiku la Sabata. Koma Yesu adaadziŵa maganizo ao, tsono adalamula munthu wopuwala dzanja uja kuti, “Tabwera, udzaime kutsogolo kuno.” Iye adanyamuka nakaima kutsogoloko. Pamenepo Yesu adauza anthu aja kuti, “Ntakufunsani, kodi Malamulo amalola chiti pa tsiku la Sabata, kuchitira munthu zabwino, kapena kumchita zoipa? Kupulumutsa moyo wa munthu, kapena kuuwononga?” Adaŵayang'ana onsewo, kenaka adalamula munthu uja kuti, “Tambalitsa dzanja lako.” Iye adalitambalitsa, ndipo dzanja lakelo lidakhalanso bwino. Koma akuluakulu aja adakwiya kwambiri, nayamba kukambirana zoti achite naye Yesu. Masiku amenewo Yesu adapita ku phiri kukapemphera, ndipo adachezera usiku wonse akupemphera kwa Mulungu. Kutacha adaitana ophunzira ake, nasankhapo khumi ndi aŵiri. Adaŵatcha “atumwi.” Anthu ake anali aŵa: Simoni (amene Yesu adamutcha dzina loti Petro) ndi mbale wake Andrea; Yakobe ndi Yohane; Filipo ndi Bartolomeo; Mateyo ndi Tomasi; Yakobe (mwana wa Alifeyo) ndi Simoni (wa m'chipani chandale cha Azelote;) Yudasi (mwana wa Yakobe) ndiponso Yudasi Iskariote (amene pambuyo pake adapereka Yesu kwa adani ake.) Yesu adatsika phiri pamodzi ndi ophunzira ake, naima pa chidikha. Panali khamu lalikulu la ophunzira ake, ndi anthu ena ambirimbiri ochokera ku dera lonse la Yudeya ndi ku Yerusalemu, ndi ku mbali yakunyanja, ku Tiro, ndi ku Sidoni. Iwo adabwera kudzamva mau ake, ndiponso kuti Iye aŵachiritse. Anthu amene ankasautsidwa ndi mizimu yoipa, amenewonso Iye ankaŵachiritsa. Anthu onsewo ankafuna kumkhudza, chifukwa mphamvu zinkatuluka mwa Iye ndi kuŵachiritsa onse. Yesu adayang'ana ophunzira ake, naŵauza kuti, “Ndinu odala, inu osaukanu, Ufumu wa Mulungu ndi wanu. “Ndinu odala, inu amene mukumva njala tsopano, chifukwa mudzakhuta. “Ndinu odala, inu amene mukulira tsopano, chifukwa mudzakondwa. “Ndinu odala anthu akamadana nanu, akamakusalani ndi kukuchitani chipongwe, ndipo akamaipitsa dzina lanu chifukwa cha Ine Mwana wa Munthu. Nthaŵi imeneyo sangalalani ndi kuvina ndi chimwemwe, chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu Kumwamba. Paja ndi zomwenso makolo ao ankaŵachita aneneri kale. “Koma ndinu atsoka, anthu achumanu, chifukwa mwalandiriratu zokusangalatsani. Ndinu atsoka, amene mukukhuta tsopanonu, chifukwa mudzamva njala. Ndinu atsoka, amene mukukondwa tsopanonu, chifukwa mudzamva chisoni ndiponso mudzalira. “Ndinu atsoka, anthu onse akamakuyamikani. Paja makolo ao ankachitira aneneri onama akale zomwezi.” “Koma inu amene mukumva mau anga, ndikukuuzani kuti, Muzikonda adani anu, muziŵachitira zabwino amene amadana nanu. Muziŵafunira madalitso amene amakutembererani, muziŵapempherera amene amakuvutitsani. Ngati munthu akumenya pa tsaya, uperekere linalonso. Ndipo munthu akakulanda mwinjiro wako, umlole atenge ndi mkanjo womwe. Munthu akakupempha kanthu, uzimpatsa. Ndipo munthu akatenga zinthu zako, usamlamule kuti abweze. Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. “Ngati mukonda okhawo amene amakukondani, mungayembekeze kulandira mphotho yanji? Pajatu ngakhale anthu ochimwa amakondanso amene amaŵakonda. Ngati muchitira zabwino okhawo amene amakuchitirani zabwino, mungayembekeze kulandira mphotho yanji? Pajatu ngakhale anthu ochimwa amachita chimodzimodzi. Ndipo ngati mukongoza okhawo amene mukudziŵa kuti adzakubwezerani, mungayembekeze kulandira mphotho yanji? Pajatu ngakhale anthu ochimwa amakongoza anzao ochimwa, kuti akalandirenso momwemo. Iyai, inu muzikonda adani anu, muzichita zabwino, ndipo muzikongoza osayembekeza kulandirapo kanthu. Mukatero mudzalandira mphotho yaikulu, ndiye kuti mudzakhala ana a Mulungu Wopambanazonse. Pajatu Iye amachitira zabwino anthu osayamika ndi oipa omwe. Monga Atate anu akumwamba ali achifundo, inunso mukhale achifundo.” “Musamaweruza anthu ena kuti ngolakwa, ndipo Mulungu sadzakuweruzani. Musamaimba ena mlandu, ndipo Mulungu sadzakuimbani mlandu. Muzikhululukira ena, ndipo Mulungu adzakukhululukirani. Muzipereka moolowa manja, ndipo Mulungu adzakuchitirani momwemo: adzakupatsirani m'thumba mwanu muyeso wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Chifukwatu muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu.” Yesu adaŵapheranso fanizo, adati, “Kodi wakhungu nkutsogolera wakhungu mnzake? Nanga onse aŵiri sadzagwa m'dzenje kodi? Wophunzira saposa mphunzitsi wake, koma aliyense pamene watsiriza maphunziro ake, adzafanafana ndi mphunzitsi wake. “Umaoneranji kachitsotso kamene kali m'maso mwa mnzako, koma osaganizako za chimtengo chimene chili m'maso mwako momwe? Ungamuuze bwanji mbale wako kuti, ‘Mbale wanga, taima ntakuchotsa kachitsotso kali m'maso mwakoka,’ pamene iweyo sukuchiwona chimtengo chimene chili m'maso mwako momwe? Iwe wachiphamaso, yamba wachotsa chimtengo m'maso mwako, pamenepo ndiye udzatha kupenya bwino nkukachotsa kachitsotso kamene kali m'maso mwa mbale wako.” “Mtengo wabwino sungabale zipatso zoipa, kapenanso mtengo woipa kubala zipatso zabwino. Mtengo uliwonse umadziŵika ndi zipatso zake. Sathyola nkhuyu pa minga, kapenanso mphesa pa mtula. Munthu wabwino amatulutsa zabwino m'chuma chabwino cha mumtima mwake. Nayenso munthu woipa amatulutsa zoipa m'chuma choipa cha mumtima mwake. Pajatu pakamwa pamalankhula zimene zadzaza mu mtima.” “Bwanji mumangoti, ‘Ambuye, Ambuye,’ koma chonsecho simuchita zimene ndimanena? Munthu aliyense wodza kwa ine, namva mau anga nkumaŵagwiritsa ntchito, ndikuuzani amene amafanafana naye. Amafanafana ndi munthu womanga nyumba, amene adaakumba mozama, naika maziko pa thanthwe. Tsono chigumula chitafika, madzi ake adagunda nyumbayo, koma sadaigwedeze, chifukwa adaaimanga bwino. Koma munthu wongomva mau anga, osaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu amene adaamanga nyumba pamwamba pa nthaka, osakumba maziko. Pamene madzi a chigumula adagunda nyumbayo, pompo idagwa, ndipo kuwonongeka kwake kunali kotheratu.” Yesu atatsiriza kulankhula zonsezi ndi anthu aja, adapita ku Kapernao. Tsono mkulu wina wa gulu la asilikali achiroma 100 anali ndi wantchito amene ankamukonda kwambiri. Wantchitoyo ankadwala, ndipo anali pafupi kufa. Mkuluyo atamva za Yesu, adatuma akulu ena a Ayuda kwa Iye kukampempha kuti adzachiritse wantchito wakeyo. Pamene adafika kwa Yesu, adampempha kolimba namuuza kuti, “Ameneyu ngwoyeneradi kuti mumchitire zimenezi, chifukwa amaukonda mtundu wathu, mwakuti adatimangira nyumba yamapemphero.” Tsono Yesu adapita nawo. Pamene Iye ankayandikira nyumba yake, mkulu wa asilikali uja adatuma abwenzi ake kwa Yesu kukamuuza kuti, “Ambuye, musadzivute, pakuti sindili woyenera kuti Inu nkuloŵa m'nyumba mwanga. Nchifukwa chake sindidadziyesenso woyenera kudza kwa Inu. Koma mungonena mau okha kuti wantchito wanga achire. Inetu ndili ndi akuluakulu ondilamulira, komanso ndili ndi asilikali amene ineyo ndimaŵalamulira. Ndimati ndikauza wina kuti, ‘Pita’, amapitadi. Ndikauzanso wina kuti, ‘Bwera’, amabweradi. Ndipo ndikauza kapolo wanga kuti, ‘Chita chakuti’, amachitadi.” Yesu atamva zimenezi, adachita naye chidwi. Adatembenuka nauza chinamtindi cha anthu amene ankamutsata aja kuti, “Ndithudi, ngakhale pakati pa Aisraele sindidapeze chikhulupiriro chotere.” Otumidwa aja adabwerera kunyumba, nakapeza wantchito uja atachiritsidwa. Pambuyo pake Yesu adapita ku mudzi wina, dzina lake Naini. Ophunzira ake pamodzi ndi anthu ena ambirimbiri adatsagana naye. Pamene Yesu ankayandikira chipata cha mudziwo, adakumana ndi anthu atanyamula maliro. Womwalirayo anali mwana wamwamuna. Mai wake wa mwanayo anali wamasiye, ndipo mwana wake anali yekhayo. Anthu ambirimbiri am'mudzimo anali naye. Pamene Ambuye adamuwona, adamumvera chisoni, namuuza kuti, “Mai, musalire.” Tsono adafika pafupi nakhudza chithathacho. Anthu amene ankanyamula malirowo adaima, ndipo Yesu adati, “Mnyamata iwe, ndikukuuza kuti, Uka.” Pamenepo wakufayo adakhala tsonga nayamba kulankhula, Yesu nkumupereka kwa mai wake. Anthu onse adachita mantha, nayamba kutamanda Mulungu. Adati, “Mneneri wamkulu waoneka pakati pathu.” Adatinso, “Mulungu wadzathandiza anthu ake.” Mbiri ya Yesuyi idawanda m'dziko lonse la Yudeya, ndi ku madera onse ozungulira. Ophunzira a Yohane adamsimbira zonsezi Yohaneyo. Tsono iye adaitanapo ophunzira ake ena aŵiri, naŵatuma kwa Ambuye kukaŵafunsa kuti, “Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” Pamene iwo adafika kwa Yesu, adamuuza kuti, “Yohane Mbatizi watituma kwa Inu kuti tidzakufunseni kuti, ‘Kodi Inuyo ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?’ ” Nthaŵi imeneyo nkuti Yesu akuchiritsa kumene nthenda zosiyanasiyana za anthu ambiri. Ankatulutsa mizimu yoipa, nkumapenyetsa anthu akhungu ambiri. Tsono Iye adayankha ophunzira a Yohane aja kuti, “Pitani, kamuuzeni Yohane zimene mwaona ndi kuzimva. Akhungu akupenya, opunduka miyendo akuyenda, akhate akuchira, agonthi akumva, akufa akuukitsidwa, ndipo amphaŵi akumva Uthenga Wabwino. Ngwodala munthu amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.” Amithenga a Yohane aja atachoka, Yesu adayamba kufunsa makamu a anthu aja za Yohane kuti, “Kodi m'mene mudaapita ku chipululu, mudaati mukaona chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi? Nanga mudaati mukaona chiyani? Munthu wovala zofeŵa kodi? Iyai, anthu ovala zakaso ndi okonda madyerero amakhala m'nyumba za mafumu. Tanenanitu, mudaati mukaona chiyani? Mneneri kodi? Zoonadi, ndipo ndikunenetsa kuti mudakaona woposa mneneri. Ameneyu ndiye uja Malembo akunena zakeyu kuti, “ ‘Nayitu nthumwi yanga, ndikuituma m'tsogolo mwako, kuti ikakonzeretu njira yodzadzeramo iwe.’ “Ndithu ndikunenetsa kuti mwa anthu onse amene adabadwa pansi pano, palibe ndi mmodzi yemwe woposa Yohane. Komabe ngakhale amene ali wamng'onong'ono mu Ufumu wa Mulungu amampambana. Anthu onse, ndi okhometsa msonkho omwe, adamva mau a Yohane, ndipo pakubatizidwa ndi Yohaneyo adavomereza kuti Mulungu ngwolungama. Koma Afarisi ndi akatswiri a Malamulo, pakukana kubatizidwa ndi iye, adakana okha zimene Mulungu adafuna kuŵachitira. “Kaya anthu amakonoŵa ndingaŵafanizire ndi chiyani? Ali ngati chiyani? Ali ngati ana okangana pa msika, ena akufunsa anzao kuti, “ ‘Tidaakuimbirani ng'oma yaukwati, bwanji inu osavina? Tidaabuma maliro, bwanji inu osalira?’ “Paja Yohane Mbatizi atabwera, ankasala zakudya ndipo sankamwa vinyo, inu nkumati, ‘Adagwidwa ndi mizimu yoipa.’ Mwana wa Munthu adabwera, nkumadya ndi kumwa ndithu, inu mumvekere, ‘Tamuwonani, munthuyu ndi wadyera, chidakwa, ndiponso bwenzi la anthu amsonkho ndi anthu osasamala Malamulo.’ Komabe chilungamo cha nzeru za Mulungu chimatsimikizika ndi zochita zake.” Wina wa m'gulu la Afarisi adaitana Yesu kuti akadye kwao. Yesu adapita nakaloŵa m'nyumba ya Mfarisiyo nkukakhala podyera. M'mudzimo mudaali mai wachiwerewere. Iyeyu atamva kuti Yesu akudya m'nyumba ya Mfarisi uja, adabwera ndi nsupa yagalasi ya mafuta onunkhira. Adakagwada kumbuyo, ku mapazi a Yesu, akulira, nayamba kukhetsera misozi pa mapazi a Yesu, nkumaŵapukuta ndi tsitsi la kumutu kwake. Adampsompsonanso mapazi akewo, naŵadzoza ndi mafuta aja. Koma Mfarisi amene adaaitana Yesu uja ataona zimenezi, adayamba kuganiza kuti, “Munthuyu akadakhaladi mneneri, bwenzi atamdziŵa mai amene akumkhudzayu, kuti ndi wachiwerewere.” Apo Yesu adamuuza kuti, “Simoni, ndili ndi nkhani yoti ndikuuze.” Iye adati, “Aphunzitsi, nenani.” Yesu adati, “Panali anthu aŵiri amene adaakongola ndalama kwa munthu wokongoza ndalama. Wina adaakongola ndalama makumi asanu, wina ndalama zisanu. Popeza kuti adaalibe choti abwezere, adaŵakhululukira ngongolezo onse aŵiri. Tsono iweyo ukuganiza kuti mwa aŵiriŵa ndani adzakonde wokongozayo koposa?” Simoni adati, “Ndiyesa koma amene adamkhululukira zambiri uja.” Yesu adamuuza kuti, “Wayankha bwino.” Atatero, Yesu adacheukira mai uja, nauza Simoni kuti, “Ukumuwona maiyu? Ine ndaloŵa m'nyumba mwako muno, iwe sudandipatse madzi otsukira mapazi anga. Koma iyeyu wakhala akukhetsera misozi pa mapazi anga, nkumaŵapukuta ndi tsitsi lake. Iwe sudandimpsomphsone, koma iyeyu chiloŵere changa muno, wakhalira kumpsompsona mapazi anga osalekeza. Iwe sudandidzoze kumutu kwanga ndi mafuta, koma iyeyu wadzoza mapazi anga ndi mafuta onunkhira. Mwakuti kunena zoona, chikondi chachikulu chimene iyeyu waonetsa, chikutsimikiza kuti Mulungu wamkhululukiradi machimo ake amene ali ochuluka. Koma munthu amene wakhululukidwa zochepa, amangokonda pang'ono.” Ndipo Yesu adauza mai uja kuti, “Machimo ako akhululukidwa.” Apo amene ankadya naye adayamba kudzifunsa mumtima mwao kuti, “Kodi ndani uyu wokhululukira ndi machimo omweyu?” Koma Yesu adauza maiyo kuti, “Chikhulupiriro chanu chakupulumutsani. Pitani ndi mtendere.” Pambuyo pake Yesu adanka nayendera mizinda ndi midzi akulalika ndi kuuza anthu Uthenga Wabwino wonena za ufumu wa Mulungu. Ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja anali naye. Panalinso azimai ena amene Yesu adaaŵatulutsa mizimu yoipa ndi kuŵachiza nthenda zina. Azimaiwo ndi aŵa: Maria, wotchedwa Magadalena, (amene mwa iye mudaatuluka mizimu yoipa isanu ndi iŵiri); Yohana, mkazi wa Kuza, kapitao wa Herode; Suzana, ndiponso azimai ena ambiri amene ndi ndalama zao ankathandiza Yesu ndi ophunzira ake. Anthu ambirimbiri ochokera ku midzi yonse adasonkhana kumene kunali Yesu. Tsono Iye adaŵaphera fanizo. Adati, “Munthu wina adaapita kukafesa mbeu. Akufesa choncho, mbeu zina zidagwera m'njira. Zidapondedwa, ndipo mbalame zidazitolatola. Mbeu zina zidagwera pa nthaka yapathanthwe. Zidamera, koma nkufota, chifukwa zidaasoŵa chinyontho. Mbeu zina zidagwera pa zitsamba zaminga. Zitsambazo pokula zidalanda chakudya cha mbeu zija. Koma mbeu zina zidagwera pa nthaka yabwino. Zidakula nkubereka. Ngala iliyonse inali ndi njere makumi khumi.” Tsono Yesu adalankhula mokweza mau kuti, “Amene ali ndi makutu akumva, amve!” Ophunzira a Yesu adamufunsa za tanthauzo la fanizoli. Tsono Iye adati, “Inuyo Mulungu adakuululirani zobisika zokhudza Ufumu wake. Koma enaŵa amazimvera m'mafanizo chabe, kuti choncho ayang'ane, koma asapenye, ndipo amve, koma asamvetse.” “Tanthauzo la fanizoli ndi ili: Mbeu zija ndi mau a Mulungu. Mbeu zogwera m'njira zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu. Koma Satana amabwera, nkuchotsa mau aja m'mitima mwao, kuwopa kuti angakhulupirire ndi kupulumuka. Mbeu zogwera pa nthaka yapathanthwe zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu, nkuŵalandira ndi chimwemwe. Tsono popeza kuti alibe mizu yozama, amangokhulupirira kanthaŵi pang'ono chabe, mwakuti pa nthaŵi ya kuyesedwa, amabwerera m'mbuyo. Mbeu zogwera pa zitsamba zaminga zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu, koma pambuyo pake nkhaŵa, kukondetsa chuma, ndiponso khumbo la zokondweretsa za moyo uno zimaŵalepheretsa, ndipo zipatso zao sizikhwima. Koma mbeu zogwera pa nthaka yabwino zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu, naŵasunga mu mtima woona ndi wabwino, ndipo amalimbikira mpaka kubereka zipatso.” “Palibe munthu amene amayatsa nyale nkuivundikira ndi mbiya, kapena kuibisa kunsi kwa bedi. Koma amaiika pa malo oonekera, kuti anthu oloŵa m'nyumba aone kuŵala kwake. Pajatu chinthu chilichonse chobisika chidzaululuka, ndipo chilichonse chachinsinsi chidzadziŵika nkuwonekera poyera. “Nchifukwa chake muzisamala m'mene mumamvera mau. Pajatu amene ali nako kanthu, adzamuwonjezera zina. Koma amene alibe kanthu, ngakhale kamene akuyesa kuti ali nakoko adzamlandabe.” Amai ake ndi abale ake a Yesu adabwera kunyumbako, koma chifukwa cha kuchuluka kwa anthu, adaalephera kufika pamene panali Iyepo. Tsono munthu wina adauza Yesu kuti, “Amai anu ndi abale anu ali panjapa, akufuna kukuwonani.” Koma Yesu adati, “Inetu amai anga ndi abale anga ndi anthu amene amamva mau a Mulungu, nkumachitadi zimene mauwo akunena.” Tsiku lina Yesu adaloŵa m'chombo pamodzi ndi ophunzira ake. Adaŵauza kuti, “Tiyeni tiwoloke, tipite ku tsidya ilo la nyanja.” Ndipo adanyamukadi. Pamene ankaoloka Yesu adagona tulo. Tsono padauka namondwe panyanjapo, mpaka chombo chija chidayamba kudzaza ndi madzi ndipo iwo anali pafupi kumira. Pamenepo ophunzira aja adadza kwa Yesu namudzutsa, adati, “Ambuye, Ambuye, tikumiratu!” Iye adadzuka, naletsa mphepoyo ndi mafunde amphamvuwo. Zidalekadi ndipo padagwa bata. Tsono Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi chikhulupiriro chanu chili kuti?” Koma iwo adaagwidwa ndi mantha nathedwa nzeru, nkumafunsana kuti, “Kodi ameneyu ndi munthu wotani? Angolamula mphepo ndi madzi omwe, izo nkumumveradi.” Iwo adafika ku dziko la Ageregesa, limene lidapenyana ndi Galileya. Pamene Yesu adafika pa mtunda, munthu wina wochokera ku mudzi wakomweko, adadzakumana naye. Munthuyo adaali ndi mizimu yoipa, ndipo kuyambira kale sankavalanso zovala. Sankakhala m'nyumba, koma ku manda. Pamene iye adaona Yesu, adafuula nadzigwetsa ku mapazi ake, ndipo adanena mokweza mau kuti, “Kodi ndakuputani chiyani Inu Yesu, Mwana wa Mulungu Wopambanazonse? Ndakupembani, musandizunze.” Adaatero chifukwa Yesu anali atalamula mzimu woipawo kuti utuluke mwa munthuyo. (Ndiye kuti kaŵirikaŵiri ukamugwira, anthu ankamumanga manja ndi maunyolo, nkumumanganso miyendo ndi zitsulo kuti amugwiritse bwino. Koma iyeyo ankazingomwetsula zomangirazo, ndipo mzimuwo unkamupirikitsira ku thengo.) Tsono Yesu adamufunsa munthuyo kuti, “Dzina lako ndani?” Iye adayankha kuti, “Dzina langa ndine Chigulu,” chifukwa mizimu yoipa yochuluka inali itamuloŵa. Kenaka mizimuyo idapempha Yesu kuti asailamule kuti ikaloŵe ku chiphompho chao. Pafupi pomwepo, pachitunda poteropo, pankadya gulu lalikulu la nkhumba. Tsono mizimu yoipa ija idapempha Yesu kuti ailole ikaloŵe m'nkhumbazo. Yesu adailoladi. Iyo idatuluka, nkukaloŵadi m'nkhumbazo. Pomwepo gulu lonselo lidaguduka kutsika chitunda chija mwaliŵiro, nkukadziponya m'nyanja, mpaka kufera m'madzimo. Oŵeta nkhumbazo ataona zimenezi, adathaŵa, nakauza anthu ku mzinda ndi ku midzi. Anthuwo adatuluka kuti akaone zimene zidaachitikazo. Atafika kumene kunali Yesuko, adapeza munthu amene adaamtulutsa mizimu yoipa uja, atakhala pansi ku mapazi a Yesu, atavala, misala ija itatha. Anthuwo adagwidwa ndi mantha. Anzao amene adaaonerera zonse zikuchitika, adaŵasimbira m'mene munthu wamizimuyo adaamchiritsira. Apo anthu onse a ku malo ozungulira Geregesa adapempha Yesu kuti achoke kumeneko, chifukwa iwo anali ndi mantha aakulu. Choncho Yesu adaloŵa m'chombo, nkumabwerera ku tsidya. Munthu amene adaamtulutsa mizimu yoipa uja adapempha Yesu kuti apite nao. Koma Yesu adamubweza namuuza kuti, “Iyai, iwe bwerera kwanu, ukafotokoze zazikulu zimene Mulungu wakuchitira.” Munthuyo adapitadi kwao nkumakalengeza mumzinda monse zazikulu zimene Yesu adaamchitira. Pamene Yesu adafikanso ku tsidya, chinamtindi cha anthu chidamchingamira, popeza kuti onse ankamudikira. Tsono kudafika munthu wina, dzina lake Yairo, amene anali mmodzi mwa akulu a nyumba yamapemphero. Iye adadzigwetsa ku mapazi a Yesu, nayamba kumdandaulira kuti apite kunyumba kwake, chifukwa mwana wake wamkazi anali pafupi kufa. Anali wa zaka khumi ndi ziŵiri, ndipo mwana anali yekhayo. Pamene Yesu ankapita kumeneko, anthu aja ankamupanikiza. Tsono panali mai wina amene adakhala akuvutika ndi matenda a msambo pa zaka khumi ndi ziŵiri. Adaamwaza chuma chake chonse kulipira asing'anga, koma panalibe ndi mmodzi yemwe wotha kumchiza. Iyeyu adafika cha kumbuyo kwa Yesu, nakhudza mphonje ya chovala chake, ndipodi nthaŵi yomweyo matenda a msambowo adaleka. Pompo Yesu adafunsa kuti, “Ndani wandikhudza?” Poti onse ankangoti, “Kaya,” Petro adati, “Aphunzitsi, anthu onseŵa akuzungulirani ndipo akukupanikizani.” Koma Yesu adati, “Iyai, wina wandikhudza ndithu. Ndazindikira kuti mphamvu zina zatuluka mwa Ine.” Pamene mai uja adaona kuti sangathenso kudzibisa, adadza monjenjemera nadzigwetsa ku mapazi a Yesu. Adafotokoza pamaso pa anthu onse aja chifukwa chimene adaakhudzira Yesu, ndiponso m'mene adachirira nthaŵi yomweyo. Apo Yesu adamuuza kuti, “Inu mwana wanga, chikhulupiriro chanu chakuchiritsani. Pitani ndi mtendere.” Yesu akulankhulabe, kudafika munthu wina kuchokera kunyumba kwa mkulu wa nyumba yamapemphero uja. Adamuuza mkuluyo kuti, “Mwana uja watsirizika. Musaŵavutenso Aphunzitsiŵa.” Yesu atamva mauwo adauza Yairo kuti, “Musaope ai, inu mungokhulupira, ndipo mwanayo akhalanso bwino.” Pamene Yesu adafika kunyumba kuja, sadalole kuti wina aliyense aloŵe naye, koma Petro, Yohane ndi Yakobe, ndiponso bambo wake wa mwanayo ndi mai wake. Anthu onse ankalira ndi kubuma. Koma Yesu adati, “Musalire, mwanayutu sadamwalire ai, ali m'tulo chabe.” Pamenepo anthuwo adayamba kumseka monyodola, chifukwa ankadziŵa kuti mwanayo wamwalira basi. Yesu adagwira mwanayo pa dzanja nanena mokweza mau kuti, “Mwana iwe, dzuka!” Pomwepo moyo wake udabwereramo, iyeyo nkudzukadi nthaŵi yomweyo. Kenaka Yesu adaŵauza kuti ampatse chakudya mtsikanayo. Makolo ake aja adazizwa kwambiri, koma Yesu adaŵalamula kuti asauze wina aliyense zimene zidaachitikazo. Yesu adaitana ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja naŵapatsa ulamuliro ndi mphamvu zotulutsira mizimu yoipa yonse ndi zochiritsira nthenda. Adaŵatuma kuti akalalike za ufumu wa Mulungu, ndi kukachiritsa anthu odwala. Adaŵauza kuti, “Musatenge kanthu pa ulendowu. Musatenge ndodo, kapena thumba lapaulendo, kapena kamba kapena ndalama. Musakhale ndi mikanjo iŵiri. Ndipo mukafikira kunyumba kwina, mukhale nao kumeneko mpaka itakwana nthaŵi yoti muchoke kumudziko. Ngati kumudzi kwina anthu sakulandirani, pochoka kumeneko musanse fumbi la kumapazi kwanu. Limeneli likhale chenjezo kwa iwowo.” Ophunzira aja adapitadi, adanka nalalika Uthenga Wabwino ku midzi yonse, nkumachiritsa anthu ponseponse. Mfumu Herode atamva zonse zimene zinkachitika zija, zidamuthetsa nzeru, chifukwa ena ankanena kuti, “Ameneyu ndi Yohane Mbatizi uja, adauka kwa akufa.” Koma ena ankanena kuti, “Iyai, ameneyu ndi Eliya, waonekanso.” Enanso ankati, “Iyai, koma ndi mmodzi mwa aneneri akale aja, wauka kwa akufa.” Herode adati, “Yohane ndiye paja ndidamdula pa khosi. Nanga uyunso ndani amene ndikumva zake zotereyu?” Choncho ankafunitsitsa kuti amuwone Yesuyo. Pamene atumwi aja adabwerako, adafotokozera Yesu zonse zimene adaachita. Tsono Iye adaŵatenga nakakhala nawo paokha ku mudzi wina, dzina lake Betsaida. Anthu ambirimbiri ataona zimenezi, adamtsatira. Iye adaŵalandira bwino nayamba kulankhula nawo za ufumu wa Mulungu, nkumachiritsa odwala. Dzuŵa lili pafupi kuloŵa, ophunzira khumi ndi aŵiri aja adadzauza Yesu kuti, “Bwanji anthuŵa azinyamuka tsopano, apite ku midzi ndi ku miraga ili pafupiyi, kuti akapeze malo ogona ndiponso chakudya, chifukwatu kuno nkuthengo.” Koma Yesu adaŵauza kuti, “Inuyo apatseni chakudya.” Iwo adati, “Tili ndi buledi msanu ndi nsomba ziŵiri zokha. Kaya kapena tipite tikaŵagulire anthu onseŵa chakudya?” Ndiye kuti amuna okha adaalipo ngati zikwi zisanu. Tsono Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Auzeni anthuŵa akhale pansi m'magulumagulu, gulu lililonse anthu ngati makumi asanu.” Ophunzira aja adaŵakhalitsadi anthu onse aja pansi. Pambuyo pake Yesu adatenga buledi msanu uja ndi nsomba ziŵiri zija, nayang'ana kumwamba, nkuthokoza Mulungu. Kenaka atanyemanyema bulediyo, adazipereka kwa ophunzira ake kuti agaŵire anthuwo. Anthu onse aja adadya nakhuta. Ndipo ophunzira aja adatola zotsala, nkudzaza madengu khumi ndi aŵiri. Nthaŵi ina pamene Yesu ankapemphera yekha, ophunzira ake adaali naye. Tsono Iye adaŵafunsa kuti, “Kodi anthu amati Ine ndine yani?” Iwo adati, “Ena amati ndinu Yohane Mbatizi, ena amati ndinu Eliya. Koma enanso amati mneneri wina wakale wauka kwa akufa.” Apo Yesu adaŵafunsa kuti, “Nanga inuyo, mumati ndine yani?” Petro adayankha kuti, “Inu ndinu Mpulumutsi wolonjezedwa uja wa Mulungu.” Yesu adalamula ophunzira ake kuti asauze munthu wina aliyense zimenezi. Adati, “Mwana wa Munthu adzayenera kuzunzidwa kwambiri. Akulu a Ayuda ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo adzamkana. Iye adzaphedwa, koma mkucha wake adzauka kwa akufa.” Pambuyo pake adauza onse amene anali pamenepo kuti, “Munthu wofuna kutsata Ine, adzikane mwiniwakeyo, ndipo asenze mtanda wake tsiku ndi tsiku nkumanditsata. Chifukwa wofuna kupulumutsa moyo wake adzautaya, koma wotaya moyo wake chifukwa cha Ine, adzaupulumutsa. Nanga ndiye kuti munthu wapindulanji atapata zonse zapansipano, iyeyo nkutaya moyo wake kapena kuuwononga? Pajatu munthu akamakana Ine ndiponso mau anga, nanenso Mwana wa Munthune ndidzamkana pamene ndidzabwera ndili ndi ulemerero wanga ndi wa Atate anga, ndi wa angelo oyera. Koma ndithu ndikunenetsa kuti alipo ena pompano omwe sadzafa asanaone Ufumu wa Mulungu utafika.” Patapita ngati masiku asanu ndi atatu atanena mau ameneŵa, Yesu adatenga Petro, Yohane ndi Yakobe, nakwera nawo ku phiri kukapemphera. Pamene Iye ankapemphera, maonekedwe a nkhope yake adasandulika, ndipo zovala zake zidachita kuti mbee kuyera. Nthaŵi yomweyo anthu aŵiri adayamba kucheza naye; anali Mose ndi Eliya. Maonekedwe ao anali aulemerero, ndipo ankakambirana za imfa ya Yesu imene ankayenera kukafera ku Yerusalemu. Nthaŵi imeneyo nkuti Petro ndi anzake ali m'tulo tofa nato. Koma pamene adadzuka, adaona ulemerero wa Yesu, ndiponso anthu aŵiri aja ali naye. Pamene iwo aja ankalekana naye, Petro adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, ndi bwino kuti ife tili nao pano. Tiloleni timange misasa itatu, wina wanu, wina wa Mose, wina wa Eliya.” (Sankadziŵa zimene ankanena.) Akulankhula choncho, padafika mtambo nuŵaphimba, ndipo ophunzirawo adagwidwa ndi mantha. Mumtambomo mudamveka mau akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndidamsankha, muzimumvera.” Mauwo atamveka choncho, ophunzira aja adaona kuti Yesu ali yekha. Iwo adangokhala chete masiku amenewo, osauza wina aliyense zimene adaaziwonazo. M'maŵa mwake Yesu ndi ophunzira atatuwo adatsika kuphiri kuja, ndipo anthu ambirimbiri adadzamchingamira. Munthu wina pakati pa anthuwo adanena mokweza mau kuti, “Aphunzitsi, chonde tandiwonerani mwana wangayu, ine mwana ndi mmodzi yemweyu. Ali ndi mzimu woipa umene umati ukamugwira, amayamba kukuwa mwadzidzidzi. Tsono ukamzunguza kolimba, mwanayu amangoti thovu tututu kukamwa. Ndipo sumusiya mpaka utampweteka ndithu. Ndinapempha ophunzira anuŵa kuti autulutse, koma alephera.” Yesu adati, “Ha! Anthu a mbadwo wopanda chikhulupiriro ndi wopotoka maganizo. Ndiyenera kukhala nanube ndi kukupirirani mpaka liti? Tabwera nayeni kuno mwana wanuyo.” Pamene mwanayo ankabwera, mzimu woipawo udamgwetsa pansi nkumuzunguza kolimba. Koma Yesu adazazira mzimu woipawo. Kenaka atamchiritsa mwanayo, adamperekanso kwa bambo wake. Apo anthu onse aja adazizwa nazo mphamvu za Mulunguzi. Pamene anthu onse aja ankazizwabe ndi zonse zimene Yesu adaachita, Iye adauza ophunzira ake kuti, “Mumvetse bwino zimene ndikuuzenizi: Mwana wa Munthu akudzaperekedwa kwa anthu.” Iwowo sadamvetse mau ameneŵa. Anali obisika kwa iwo, kotero kuti sadaŵamvetsetse. Koma ankaopa kumufunsa zimenezi. Ophunzira adayamba kutsutsana zakuti wamkulu ndani pakati pao. Koma Yesu adaadziŵa zimene zinali kukhosi kwao. Tsono adatenga mwana, namukhazika pambali pake. Ndiye adaŵauza kuti, “Aliyense wolandira bwino mwanayu chifukwa cha Ine, ndiye kuti akulandira bwino Ine amene. Ndipo wondilandira Ine bwino, ndiye kuti akulandira bwino Atate amene adandituma. Pakuti amene simukumuyesa kanthu pakati pa inu nonse, ameneyo ndiye wamkulu.” Yohane adati, “Aphunzitsi, ife tinaona munthu wina akutulutsa mizimu yoipa potchula dzina lanu, ndiye ife tinayesa kumletsa, chifukwa sayenda nafe.” Koma Yesu adamuuza kuti, “Musamletse ai, chifukwa wosatsutsana nanu, ngwogwirizana nanu ameneyo.” Pamene masiku ankayandikira oti Yesu atengedwe kunka Kumwamba, Iye adatsimikiza ndithu zopita ku Yerusalemu. Motero adatuma amithenga kuti atsogole, akaloŵe m'mudzi wina wa Asamariya kukamkonzera malo. Koma anthu am'mudzimo sadafune kumlandira, chifukwa Iye ankapita ku Yerusalemu. Ophunzira ake, Yakobe ndi Yohane ataona zimenezi adati, “Ambuye, bwanji tiitane moto kuchokera Kumwamba kuti udzaŵapsereze anthu ameneŵa?” Koma Yesu adacheuka nadzudzula ophunzirawo. Pambuyo pake onse pamodzi adapita ku mudzi wina. Pamene iwo anali panjira, munthu wina adauza Yesu kuti, “Ndizikutsatani kulikonse kumene muzipita.” Yesu adamuyankha kuti, “Nkhandwe zili ndi michembo yake, mbalame zili ndi zisa zake, koma Mwana wa Munthu alibe mpogoneka mutu pomwe.” Pambuyo pake Yesu adauza munthu wina kuti, “Iwe, unditsate!” Iyeyo adati, “Ambuye, mundilole ndiyambe ndakaika maliro a atate anga.” Yesu adamuuza kuti, “Aleke akufa aziika akufa anzao. Koma iwe, kalalike Ufumu wa Mulungu.” Munthu winanso adauza Yesu kuti, “Ndidzakutsatani, Ambuye, koma mundilole ndiyambe ndakatsazikana ndi anthu kunyumba.” Yesu adati, “Munthu amene wayambapo kulima, tsono nkumachewukiranso kumbuyo, Mulungu alibe naye ntchito mu Ufumu wake.” Pambuyo pake Ambuye adasankha anthu 72, naŵatuma aŵiriaŵiri kuti atsogole kupita ku mudzi uliwonse ndi ku malo aliwonse kumene Iye ankati apiteko. Adaŵauza kuti, “Dzinthu ndzambiri, koma antchito ngochepa. Nchifukwa chake pemphani Mwini dzinthu kuti atume antchito kukatuta dzinthudzo. Pitani tsono. Ndikukutumani ngati anaankhosa pakati pa mimbulu. Musatenge chikwama cha ndalama, kapena thumba lapaulendo, kapenanso nsapato zapadera ai. Musaimenso kuti mupereke moni pa njira. Kunyumba kulikonse kumene mukaloŵe, muyambe mwanena kuti, ‘Mtendere ukhale m'nyumba muno.’ Ngati m'nyumbamo muli munthu wofuna mtendere, mtendere umene mwanenawo udzakhala pa iyeyo. Koma ngati mulibe munthu wofuna mtendere, mtendere umene mwanenawo udzabwerera kwa inu. Khalani m'nyumba yomweyo. Mudye ndi kumwa zimene akupatsani, pakuti wantchito ngwoyenera kulandira malipiro ake. Musamachoka kumene mwafikirako nkukaloŵa ku nyumba zina ai. Mukaloŵa m'mudzi, anthu nakulandirani, mudye zimene akukonzerani. Muchiritse anthu odwala amene ali m'mudzimo, ndipo muŵauze kuti, ‘Tsopano ufumu wa Mulungu wakufikirani.’ Koma kumudzi kumene mukaloŵe, anthu nkupanda kukulandirani bwino, mukapite m'miseu yam'mudzimo, nkukanena kuti, ‘Tikukusansirani ngakhale fumbi la m'mudzi mwanu muno limene linamamatira ku mapazi athu. Komabe dziŵani kuti ufumu wa Mulungu wafika.’ Kunena zoona, pa tsiku lachiweruzo, Mulungu adzachitako chifundo polanga Sodomu koposa polanga mudzi umenewo. “Uli ndi tsoka, iwe Korazini! Uli ndi tsoka, iwe Betsaida! Chifukwa zamphamvu zimene zidachitika mwa inu, achikhala zidaachitikira ku Tiro ndi ku Sidoni, bwenzi anthu ake atavala kale ziguduli nkudzithira phulusa, kuwonetsa kuti atembenukadi mtima. Koma pa tsiku lachiweruzo, Mulungu adzachitako chifundo polanga Tiro ndi Sidoni, koposa polanga inu. Ndipo iwe Kapernao, kodi ukuyesa kuti adzakukweza mpaka Kumwamba? Iyai, adzakutsitsa mpaka ku Malo a anthu akufa.” Yesu adauza anthu 72 aja kuti, “Wokumverani inu, akumvera Ine amene. Wokukanani inu akukana Ine amene. Ndipo wondikana Ine, akukananso Atate amene adandituma.” Anthu 72 aja adabwerako ndi chimwemwe nati, “Ambuye, ngakhale mizimu yoipa yomwe imatigonjera tikamailamula m'dzina lanu.” Yesu adaŵauza kuti, “Ndidaona Satana alikugwa ngati mphezi kuchokera Kumwamba. Ndakupatsanitu mphamvu kuti muziponda njoka ndi zinkhanira, ndi kumagonjetsa mphamvu zonse za mdani uja. Palibe kanthu kamene kangakupwetekeni. Komabe musakondwere chifukwa choti mizimu yoipa ikukugonjerani, koma muzikondwera kuti maina anu adalembedwa Kumwamba.” Nthaŵi yomweyo Mzimu Woyera adadzaza Yesu ndi chimwemwe, mwakuti Yesuyo adati, “Atate, Mwini kumwamba ndi dziko lapansi, ndikukuyamikani kuti zinthuzi mudaululira anthu osaphunzira nkubisira anthu anzeru ndi ophunzira. Chabwino Atate, pakuti mudafuna kutero mwa kukoma mtima kwanu. “Atate adaika zonse m'manja mwanga. Palibe wina wodziŵa Mwana kupatula Atate okha. Palibenso wina wodziŵa Atate kupatula Mwana yekha, ndiponso amene Mwanayo akufuna kumuululira.” Pambuyo pake Yesu adatembenukira ophunzira ake, naŵauza iwo okha kuti, “Ngodala maso amene akuwona zimene mukuwonazi. Kunena zoona aneneri ambiri ndi mafumu ambiri adaafunitsitsa kuwona zimene inu mukupenyazi, koma sadaziwone. Adaafunitsitsa kumva zimene inu mukumvazi, koma sadazimve.” Katswiri wina wa Malamulo adaimirira kuti ayese Yesu. Adamufunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi ndichite chiyani kuti ndikhale ndi moyo wosatha?” Yesu adati, “Kodi m'Malamulo mudalembedwa chiyani? Mumaŵerengamo zotani?” Iye adayankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse, ndi nzeru zako zonse, ndiponso mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.” Yesu adati, “Mwayankha bwino. Kachiteni zimenezi ndipo mudzakhala ndi moyo.” Koma munthu uja pofuna kudziwonetsa ngati wolungama, adafunsa Yesu kuti, “Nanga mnzangayo ndani?” Apo Yesu adati, “Munthu wina ankatsikira ku Yeriko kuchokera ku Yerusalemu. Pa njira achifwamba adamgwira. Adamuvula zovala, nammenya, nkumusiya ali thasa, ali pafupi kufa. “Ndiye zidangochitika kuti wansembe wina ankapita pa njira yomweyo. Pamene adaona munthu uja, adangolambalala. Chimodzimodzinso Mlevi wina adafika pamalopo, ndipo pamene adaona munthuyo, nayenso adangolambalala. Koma Msamariya wina, ali pa ulendo wake, adafikanso pamalo pomwepo. Pamene adaona munthu uja, adamumvera chisoni. Adabwera kwa wovulalayo, nathira mafuta ndi vinyo pa mabala ake, nkuŵamanga. Atatero adamkweza pa bulu wake, nkupita naye ku nyumba ya alendo, namsamalira bwino. M'maŵa mwake adatulutsa ndalama ziŵiri zasiliva, nazipereka kwa mwini nyumba ya alendoyo. Adamuuza kuti, ‘Msamalireni bwino, ndipo mukamwazanso ndalama zina, ndidzakubwezerani pobwera.’ ” Tsono Yesu adafunsa katswiri wa Malamulo uja kuti, “Inu pamenepa mukuganiza bwanji? Mwa anthu atatuŵa, ndani adakhala ngati mnzake wa munthu uja achifwamba adaamugwirayu?” Iye adati, “Amene adamchitira chifundo uja.” Apo Yesu adamuuza kuti, “Pitani tsono, nanunso muzikachita chimodzimodzi.” Pamene Yesu ndi ophunzira ake anali pa ulendo wao, Iye adaloŵa m'mudzi wina. Tsono mai wina, dzina lake Marita, adamlandira kunyumba kwake. Iyeyu anali ndi mng'ono wake, dzina lake Maria, amene adaadzakhala pansi ku mapazi a Ambuye, namamva mau ake. Koma Marita ankatanganidwa ndi ntchito zambiri. Choncho adapita kwa Yesu nati, “Ambuye, kodi simukusamalako kuti mng'ono wangayu akundilekera ndekha ntchito? Muuzeni adzandithandize.” Ambuye adati, “Iwe Marita iwe, ukutekeseka nkuvutika ndi zinthu zambiri, koma chofunika nchimodzi chokha. Maria ndiye wasankhula chinthu chopambana, ndipo chimenechi palibe wina angamlande ai.” Nthaŵi ina Yesu ankapemphera pamalo pena. Pamene adatsiriza, wophunzira wake wina adampempha kuti, “Ambuye, tiphunzitseni kupemphera, monga Yohane Mbatizi adaphunzitsira ophunzira ake.” Yesu adati, “Pamene mukupemphera muziti, “ ‘Atate, dzina lanu lilemekezedwe. Ufumu wanu udze. Mutipatse ife tsiku lililonse chakudya chathu chamasikuwonse. Mutikhululukire ife machimo athu, pakuti ifenso timakhululukira aliyense wotilakwira. Ndipo musalole kuti tigwe m'zotiyesa.’ ” Adaŵauzanso kuti, “Tangoganizani: wina mwa inu ali ndi bwenzi lake, nkupita kunyumba kwake pakati pa usiku, nakamuuza kuti, ‘Iwe mnzanga, kodi ungakhale ndi buledi mtatu? Kwafika bwenzi langa, ali pa ulendo, ndipo ndilibe choti ndingampatse.’ Koma wam'nyumbayo nkuyankha kuti, ‘Usandivute, ndatseka kale pa khomo, ndipo ine ndi ana anga tagona, sindingadzukenso kuti ndikupatse bulediyo.’ Ndithu ndikunenetsa kuti adzauka nkumupatsa, osati chifukwa ndi bwenzi lake, koma chifukwa cha khama la wopempha uja. Ndipo adzampatsa zonse zimene akusoŵa. “Motero ndikukuuzani kuti, Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza. Gogodani, ndipo adzakutsekulirani. Paja munthu amene amapempha, ndiye amalandira, amene amafunafuna, ndiye amapeza, ndipo amene amagogoda, ndiye amamtsekulira. Ndani mwa atatenu, mwana wake atampempha nsomba, iye nkumupatsa njoka? Kapena atampempha dzira, iye nkumupatsa chinkhanira? Tsono ngati inu, nkuipa kwanuku, mumadziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanji Atate akumwamba, angalephere bwanji kupereka Mzimu Woyera kwa amene aŵapempha.” Tsiku lina Yesu ankatulutsa mzimu woipa woletsa munthu kulankhula. Mzimuwo utatuluka, munthu amene anali wosalankhulayo adayamba kulankhula, mwakuti anthu ambirimbiri amene anali pomwepo adazizwa kwabasi. Koma ena mwa iwo adati, “Mphamvu zimene iyeyu amatulutsira mizimu yoipazi nzochokera kwa Belezebulu, mkulu wa mizimu yoipayo.” Enanso pofuna kumuyesa, adampempha kuti aŵaonetse chizindikiro chozizwitsa chochokera kumwamba. Koma Yesu adaadziŵa maganizo ao, motero adaŵauza kuti, “Anthu a mu ufumu uliwonse akayamba kuukirana, ufumuwo kutha kwake nkomweko. Ndipo m'banja akayamba kukangana, banjalo limapasuka. Tsono ngati a mu ufumu wa Satana ayamba kuukirana, Satanayo ufumu wake ungalimbe bwanji? Paja inu mukuti Ine ndimatulutsa mizimu yoipa ndi mphamvu za Belezebulu. Ngati Ineyo ndimatulutsa mizimu yoipa ndi mphamvu za Belezebulu, nanga ophunzira anu amaitulutsa ndi mphamvu za yani? Nchifukwa chake ophunzira anu omwewo ndi amene adzakuweruzani kuti ndinu olakwa. Koma ngati Ine ndimatulutsa mizimu yoipa ndi mphamvu za Mulungu, ndiye kuti Mulungu wayamba kukhazikitsa ufumu wake pakati panu. “Munthu wamphamvu akamalonda nyumba yake ali ndi zida zankhondo, katundu wake amakhala pabwino. Koma pakabwera wina wamphamvu zoposa, namgonjetsa, amalanda zida zimene ankazidalirazo, nkugaŵagaŵa katundu amene walandayo. “Munthu wosavomerezana ndi Ine, ndiye kuti ngwotsutsana nane. Ndipo wosandithandiza kusonkhanitsa, ndiye kuti ameneyo ngwomwaza. “Mzimu woipa ukatuluka mwa munthu, umakayendayenda ku malo opanda madzi, kufunafuna malo opumulirako. Ndipo ukapanda kuŵapeza, umati, ‘Ndibwerera kunyumba kwanga komwe ndidatuluka kuja.’ Tsono ukafika, umapeza m'nyumba muja muli mosesasesa ndi mokonza bwino. Pamenepo umakatenga mizimu ina isanu ndi iŵiri yoipa koposa uwowo, kenaka yonseyo imaloŵa nkukhazikika momwemo. Choncho mkhalidwe wotsiriza wa munthu uja umaipa koposa mkhalidwe wake woyamba.” Pamene Yesu ankalankhula zimenezi, mai wina pakati pa anthu ambiri aja adakweza mau namuuza kuti, “Ngwodala mai amene adabalani nkukuyamwitsani.” Koma Yesu adati, “Iyai, odala ndi anthu amene amamva mau a Mulungu naŵagwiritsa ntchito.” Pamene anthu ankachulukirachulukira, Yesu adati, “Anthu a mbadwo uno ngoipa, amafuna kuwona chizindikiro chozizwitsa. Komabe sadzachiwona chizindikirocho, kupatula cha mneneri Yona chija. Monga Yona uja anali chizindikiro kwa anthu a ku Ninive, chomwechonso Mwana wa Munthu adzakhala chizindikiro kwa anthu a mbadwo uno. Pa tsiku lachiweruzo mfumukazi yakumwera ija idzauka pamodzi ndi anthu a mbadwo uno, nidzaŵatsutsa. Paja iyo idaachita kuchokera ku mathero a dziko lapansi kudzamva zolankhula zanzeru za mfumu Solomoni. Ndipotu pano pali woposa Solomoni amene. Pa tsiku lachiweruzo anthu a ku Ninive aja adzauka pamodzi ndi anthu a mbadwo uno, nadzaŵatsutsa. Paja iwowo adaatembenuka mtima, atamva malaliko a Yona. Ndipotu pano pali woposa Yona amene.” “Munthu sati akayatsa nyale, nkuiika m'chipinda chapansi kapena kuivundikira ndi mbiya. Koma amaiika pa malo oonekera, kuti anthu oloŵa m'nyumbamo aone kuŵala kwake. Maso ndiwo nyale zounikira thupi lako. Ngati maso ako ali bwino, m'thupi mwako monse mumakhala kuŵala. Koma ngati maso ako sali bwino, m'thupi mwako monse mumakhala mdima. Chenjera tsono kuti kuŵala kumene kuli mwa iwe kusasanduke mdima. Ngati kuŵala kukhala m'thupi monse, popanda mdima pena paliponse, apo thupi lonse lidzakhala loŵala, monga pamene nyale ikukuunikira ndi kuŵala kwake.” Pamene Yesu adatsiriza kulankhula, wina wa m'gulu la Afarisi adamuitana kuti akadye naye. Tsono Yesu adaloŵa m'nyumba nakakhala podyera. Mfarisiyo adadabwa poona kuti Yesu wayamba kudya osatsata mwambo wao wa kasambidwe ka m'manja. Koma Ambuye adamuuza kuti, “Inu Afarisi mumatsuka kunja kwa chikho ndi mbale, koma m'kati ndinu odzaza ndi zonyenga ndi zankhanza. Ndinu anthu opusa! Kodi Mulungu amene adapanga zakunja, si yemweyo adapanganso zam'kati? Popereka zachifundo kwa amphaŵi, muzipereka zimene zili m'kati, ndiye pamenepo zanu zonse zidzakhala zoyera. “Muli ndi tsoka, inu Afarisi, chifukwa mumapereka chachikhumi cha timbeu tonunkhira, cha timbeu tokometsera chakudya, ndiponso cha mbeu zakudimba za mtundu uliwonse. Koma simulabadako kuchita chilungamo, kapena kukonda Mulungu. Mukadayenera kuchitadi zimenezi, komabe osasiya zinazo. Muli ndi tsoka, inu Afarisi, chifukwa mumakonda mipando yaulemu m'nyumba zamapemphero, ndiponso kuti anthu azikupatsani moni waulemu pa misika. Muli ndi tsoka, chifukwa muli ngati manda osazindikirika, amene anthu amapondapo osadziŵa kanthu.” Apo katswiri wina wa Malamulo adati, “Aphunzitsi, mukamanena zimenezi, mukunyozatu ndi ife tomwe.” Yesu adati, “Muli ndi tsokanso, inu akatswiri a Malamulo, chifukwa mumasenzetsa anthu katundu wosautsa kunyamula, pamene inuyo simumkhudzako mpang'ono pomwe. Muli ndi tsoka, chifukwa mumamanga ziliza za aneneri, pamene ndi makolo anu omwe akale amene adapha aneneriwo. Apo mukutsimikiza kuti mukuvomereza ntchito za makolo anuwo, popeza kuti iwowo adapha aneneriwo, inuyo nkumamanga ziliza zao. Nchifukwa chake Nzeru ya Mulungu idati, ‘Ndidzaŵatumizira aneneri ndi atumwi, koma anthu adzapha ena mwa iwo, nkuzunza ena.’ Motero anthu amakono adzakhala ndi mlandu chifukwa cha aneneri onse amene adaphedwa chilengedwere dziko lapansi, kuyambira kuphedwa kwa Abele, mpaka kuphedwa kwa Zakariya amene adaphedwera m'Nyumba ya Mulungu pakati pa guwa la nsembe ndi malo opatulika kopambana. Ndithu ndikunenetsa kuti anthu amakono adzakhaladi ndi mlandu chifukwa cha ophedwawo. “Muli ndi tsoka, inu akatswiri a Malamulo, chifukwa mudalanda kiyi yotsekulira anthu nzeru. Inu nomwe sumudaloŵe, ndipo mudatsekereza amene ankafuna kuloŵa.” Pamene Yesu adatuluka m'nyumbamo, aphunzitsi a Malamulo pamodzi ndi Afarisi adayamba kumzonda ndi kumpanikiza ndi mafunso ambiri ozunguza. Cholinga chao chinali chofuna kumtapa m'kamwa. Nthaŵi imeneyo nkuti chikhamu cha anthu zikwi ndi zikwi chikusonkhana, kotero kuti anthuwo ankangopondana. Yesu adayamba kulankhula ndi ophunzira ake poyamba, Adati, “Chenjerani ndi chofufumitsira buledi cha Afarisi, chimene chili chiphamaso. Kanthu kalikonse kovundikirika kadzaululuka, ndipo kalikonse kobisika kadzadziŵika. Nchifukwa chake zonse zimene mwalankhula pa mdima, zidzamveka poyera, ndipo zonse zimene mwanong'oneza anthu m'kati mwa nyumba, adzazilengeza pa bwalo.” “Ndikukuuzani inu, abwenzi anga, kuti musamaopa anthu. Iwo angathe kupha thupi lokha, koma pambuyo pake alibenso china choti angachitepo. Koma ndikuchenjezeni: amene muyenera kumuwopa ndi Mulungu. Iye atalanda moyo wa munthu, ali nazonso mphamvu za kumponya m'Gehena. Ndithu ndi ameneyo amene muzimuwopa. “Suja amagulitsa atimba asanu tindalama tiŵiri? Komabe Mulungu saiŵala ndi mmodzi yemwe. Ndipo tsitsi lomwe la kumutu kwanu adaliŵerenga lonse. Choncho musati muziwopa ai. Ndinu a mtengo woposa atimba ambiri.” “Ndithu kunena zoona, aliyense wondivomereza pamaso pa anthu, Inenso Mwana wa Munthune ndidzamuvomereza pamaso pa angelo a Mulungu. Koma aliyense wondikana pamaso pa anthu kuti sandidziŵa, Inenso Mwana wa Munthune ndidzamkana pamaso pa angelo a Mulungu kuti sindimdziŵa. “Aliyense wonenera zoipa Mwana wa Munthu, Mulungu adzamkhululukira, koma wonyoza Mzimu Woyera ndi mau achipongwe, Mulungu sadzamkhululukira. “Akadzakutengerani ku milandu ku nyumba zamapemphero, kapena kwa mafumu ndiponso kwa akulu a Boma, musati mudzavutike nkumati, ‘Kaya ndikayankha bwanji? Ndikanena chiyani?’ Popeza kuti Mzimu Woyera adzakudziŵitsani pa nthaŵi yomweyo zimene mudzayenera kunena.” Munthu wina pakati pa anthu onse aja adapempha Yesu kuti, “Aphunzitsi, takandiwuzirani mbale wanga kuti andigaŵireko chuma chamasiye.” Koma Yesu adati, “Munthu iwe, ndani adandipatsa ntchito yokuweruzani kapena kumakugaŵirani chuma chanu chamasiye?” Atatero adauza anthu aja kuti, “Chenjerani, ndipo mupewe khumbo lililonse lofuna zambiri. Pajatu ngakhale munthu akhale ndi chuma chochuluka chotani, chumacho sichingatchinjirize moyo wake.” Tsono Yesu adaŵaphera fanizo. Adati, “Munthu wina wachuma m'munda mwake mudabereka dzinthu dzambiri. Ndiye iye uja adayamba kuganiza kuti, ‘Nditani, poti ndilibe mosungira dzinthu dzanga?’ Tsono adati, ‘Ndidzatere: ndidzapasula nkhokwe zanga nkumanga zina zazikulu, ndipo ndidzasungira dzinthu dzanja dzonse ndi chuma changa m'menemo. Kenaka ndidzauza mtima wanga kuti, Iwe mtima wanga, uli ndi chuma chambiri chimene chidzakukwanira zaka zambiri. Upumule, uzidya, uzimwa ndi kusangalala!’ Koma Mulungu adamuuza kuti, ‘Wopusawe! Usiku womwe uno akulanda moyo wako. Nanga zonse zimene wadzisungirazi zidzakhala za yani?’ ” Potsiriza Yesu adati, “Zimatero ndi munthu amene amadziwunjikira chuma, koma sali wachuma konse pamaso pa Mulungu.” Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti musamadera nkhaŵa moyo wanu, kuti mudzadyanji, kapena thupi lanu, kuti mudzavalanji. Pakuti moyo umaposa chakudya, ndipo thupi limaposa zovala. Onani makwangwala. Safesa, sakolola, alibe nyumba yosungiramo zinthu, kapena nkhokwe, komabe Mulungu amaŵadyetsa. Inu mumazipambana mbalamezo kutali. Ndani mwa inu ndi maganizo ankhaŵa angathe kuwonjezera ngakhale tsiku limodzi pa moyo wake? Tsono ngati simungathe kuchita ngakhale kanthu kakang'ono kotere, bwanji mukudera nkhaŵa zinazo? Onani maluŵa m'mene amakulira. Sagwira ntchito kapena kuwomba nsalu ai. Komatu kunena zoona, ngakhale mfumu Solomoni yemwe, mu ulemerero wake wonse, sankavala zokongola kulingana ndi limodzi lomwe mwa maluŵa ameneŵa. Tsono ngati Mulungu amaveka motere udzu wakuthengo, umene ungokhalapo lero lokha, maŵa lino nkuponyedwa pa moto, nanji inuyo, angapande kukuvekani, inu a chikhulupiriro chochepanu? Nchifukwa chake musamadera nkhaŵa ndi kufunafuna zoti mudye, kapena zoti mumwe. Paja zimenezi amazifunafuna ndi anthu a mitundu yonse yapansipano. Atate anu amadziŵa kuti mumazisoŵa zimenezi. Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.” “Inu nkhosa zanga, ngakhale muli oŵerengeka, musaope, pakuti kudakomera Atate anu kuti akupatseni Ufumu wake. Gulitsani zonse zimene muli nazo, ndipo ndalama zake mupatse amphaŵi. Mudzipezere matumba a ndalama amene safwifwa, ndi kudziwunjikira chuma chokhalitsa Kumwamba; kumeneko mbala sizingafikeko, ndipo njenjete sizingachiwononge. Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko.” “Khalani okonzeka kutumikira, ndipo nyale zanu zikhale zoyaka. Khalani ngati antchito amene akudikira mbuye wao wochokera ku phwando la ukwati, kuti pamene afike ndi kugogoda, iwo amtsekulire msanga. Ngodala antchito amene mbuye wao pofika, aŵapeza ali maso. Ndithu ndikunenetsa kuti adzadzikonzekera, nadzaŵakhazika podyera, ndipo adzabwera nkumaŵatumikira. Ngodala antchitowo mbuye waoyo akadzaŵapeza ali choncho pamene iye adzafike, ngakhale pakati pa usiku kapena kuli pafupi kucha. “Koma kumbukirani kuti, mwini nyumba akadadziŵiratu nthaŵi yoti mbala ifika, sibwenzi atalola kuti ithyole nyumba yake. Choncho inunso khalani okonzeka, pakuti Mwana wa Munthu adzabwera pa nthaŵi imene simukuyembekeza.” Pamenepo Petro adati, “Ambuye, kodi fanizoli mukuphera ife tokha, kapena mukuuza onse?” Yesu adati, “Tsono kapitao wokhulupirika ndi wanzeru ndani, amene mbuye wake adzamuike kuti aziyang'anira onse a m'nyumba mwake, nkumaŵagaŵira chakudya chao pa nthaŵi yake? Ngwodala wantchito ameneyo, ngati mbuye wake pofika adzampeza akuchitadi zimenezi. Ndithu ndikunenetsa kuti adzamuika woyang'anira chuma chake chonse. “Koma ngati ndi wantchito woipa, mumtima mwake azidzati, ‘Mbuye wanga akuchedwa kubwera.’ Ndiye adzayamba kumenya antchito anzake, amuna ndi akazi, ndiponso kumadya, kumamwa ndi kuledzera. Tsono mbuye wake adzangoti mbwe mwadzidzidzi, pa tsiku limene iye sakumuyembekeza. Choncho adzamlanga koopsa, ndipo adzamtaya ku malo a anthu osakhulupirika. “Wantchito amene akudziŵa zimene mbuye wake amafuna, koma osakonzekera kuzichita, adzamkwapula kwambiri. Koma wantchito amene sadziŵa zimene mbuye wake amafuna, tsono nkumachita zoyenera kumlanga nazo, adzamkwapula pang'ono. Aliyense amene adalandira zambiri, adzayenera kubweza zambiri. Ndipo amene adamsungiza zambiri, adzamlamula kuti abweze zochuluka koposa.” “Ndidabwera kudzaponya moto pa dziko lapansi, ndipo ndikadakonda utayaka kale. Koma ndiyenera kuyamba ndaloŵa m'masautso akulu, ndipo mtima wanga sukhazikika mpaka zitachitika. Kodi mukuyesa kuti ndidadzapereka mtendere pansi pano? Iyai, kunena zoona, osati mtendere koma kugaŵikana. Kuyambira tsopano m'banja limodzi mudzakhala anthu asanu ogaŵikana, atatu adzakangana ndi aŵiri, ndipo aŵiri adzakangana ndi atatu. Bambo adzakangana ndi mwana wake wamwamuna, mwana wamwamuna adzakangana ndi bambo wake. Mai adzakangana ndi mwana wake wamkazi, mwana wamkazi adzakangana ndi mai wake. Apongozi adzakangana ndi mkazi wa mwana wao, ndipo mkaziyo adzakangana ndi apongozi akewo.” Yesu adauzanso anthu onse aja kuti, “Mukaona mtambo ukukwera kuzambwe, pompo mumati, ‘Mvula ikubwera,’ ndipo imabweradi. Mphepo yakumwera ikamaomba, mumati, ‘Kutentha,’ ndipo kumatenthadi. Inu anthu achiphamaso, mumatha kuzindikira maonekedwe a dziko lapansi ndi a kuthambo, koma bwanji simutha kuzindikira tanthauzo la zimene zikuchitika masiku omwe ano?” “Bwanji simutsimikiza nokha zoyenera kuchita? Monga pamene ukupita ndi mnzako wamlandu kwa woweruza, uyesetse kukonza mlanduwo mukali pa njira, kuwopa kuti angakupereke kwa woweruza, woweruzayo angakakupereke kwa msilikali, ndipo msilikaliyo angakakuponye m'ndende. Ndithu ndikunenetsa kuti sudzatulukamo mpaka utalipira zonse.” Anthu ena amene anali pomwepo adadza kwa Yesu, nayamba kumsimbira za Agalileya amene Pilato adaalamula kuti aphedwe, pamene iwo ankapereka nsembe zao kwa Mulungu. Tsono Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi mukuyesa kuti Agalileyawo anali ochimwa koposa Agalileya ena onse, popeza kuti adaphedwa motere? Iyai, koma mukapanda kutembenuka mtima, inunso mudzaonongedwa ngati iwo aja. Nanga anthu aja 18 amene nyumba yosanja idaŵagwera ku Siloamu nkuŵapha? Kodi mukuyesa kuti iwowo anali ophwanya malamulo koposa anthu ena onse okhala m'Yerusalemu? Iyai, koma mukapanda kutembenuka mtima, inunso mudzaonongedwa ngati iwo aja.” Yesu adaŵaphera fanizo, adati, “Munthu wina anali ndi mkuyu wobzalidwa m'munda wake wamphesa. Adakafunamo zipatso, koma osazipeza. Tsono adauza wosamala mundawo kuti, ‘Papita zaka zitatu tsopano ndikufuna zipatso mu mkuyu uwu, koma osazipeza. Udule tsono. Ukugugitsiranji nthaka?’ Koma iye adati, ‘Ambuye, baulekani chaka chino chokha. Ndiukumbira pa tsinde nkuuthira manyowa. Ukadzabala zipatso chaka chamaŵa, zidzakhala bwino. Koma ukakapanda kubala, apo mudzaudule.’ ” Tsiku lina la Sabata Yesu ankaphunzitsa m'nyumba ina yamapemphero. M'menemo munali mai wina amene anali ndi mzimu woipa umene udamudwalitsa zaka 18. Anali ndi msana wokhota, mwakuti sankatha konse kuŵeramuka. Pamene Yesu adamuwona, adamuitana namuuza kuti, “Mai inu, mwamasuka ku matenda anu.” Adamsanjika manja, ndipo pompo maiyo adaongoka, nayamba kutamanda Mulungu. Koma mkulu wa nyumba yamapemphero ija adakwiya, poona kuti Yesu wachiritsa munthu pa tsiku la Sabata. Tsono mkuluyo adauza anthu onse kuti, “Pali masiku asanu ndi limodzi antchito. Muzibwera masiku ameneŵa kudzachiritsidwa, osati pa tsiku la Sabata ai” Koma Ambuye adati, “Anthu achiphamaso inu, kodi suja nonsenu mumamasula ng'ombe zanu kapena abulu anu pa tsiku la Sabata kukaŵamwetsa madzi? Nanga maiyu, amene ali mwana wa Abrahamu, ndipo Satana adaamumanga zaka 18, kodi sikunayenera kuti amasulidwe ku nsinga imeneyi pa tsiku la Sabata?” Yesu atanena zimenezi, adani ake onse adachita manyazi. Koma anthu ena onse adakondwera chifukwa cha ntchito zodabwitsa zimene Iye ankachita. Yesu adati, “Kodi Ufumu wa Mulungu uli ngati chiyani, ndipo ndingauyerekeze ndi chiyani? Uli ngati njere ya mbeu ya mpiru imene munthu adakaifesa m'munda mwake. Idamera nisanduka mtengo, mbalame zamumlengalenga nkumabwera kudzamanga zisa pa nthambi zake.” Yesu adatinso, “Ndingayerekezenso ndi chiyani Ufumu wa Mulungu? Ulinso ngati chofufumitsira buledi, chimene mai wina adachisanganiza ndi ufa wokwanira miyeso itatu, mpaka mtanda wonse udafufuma.” Pa ulendo wake wopita ku Yerusalemu, Yesu ankayendera mizinda ndi midzi akuphunzitsa. Munthu wina adamufunsa kuti, “Ambuye, kodi adzapulumuka ndi anthu oŵerengeka okha?” Yesu adayankha kuti, “Yesetsani kuloŵera pa khomo lophaphatiza, pakuti kunena zoona anthu ambiri adzafuna kuloŵa, koma adzalephera. “Mwini nyumba adzanyamuka nkutseka pa khomo. Pamenepo, okhala panjanu mudzayamba kugogoda nkumanena kuti, ‘Ambuye, titsekulireni.’ Koma Iye adzakuyankhani kuti, ‘Sindikudziŵa kumene mukuchokera.’ Apo inuyo mudzayamba kunena kuti, ‘Pajatu tinkadya ndi kumamwa nanu pamodzi, ndipo Inuyo munkaphunzitsa m'miseu ya m'mizinda mwathu.’ Koma Iye adzakuuzani kuti, ‘Pepani, sindikudziŵa kumene mukuchokera. Chokani apa nonsenu, anthu ochita zoipa.’ Apo mudzayamba kulira ndi kukukuta mano, pamene mudzaona Abrahamu ndi Isaki ndi Yakobe ndi aneneri onse mu Ufumu wa Mulungu, inuyo mukuponyedwa kunja. Anthu adzachokera kuvuma ndi kuzambwe, kumpoto ndi kumwera, nadzakhala podyera mu Ufumu wa Mulungu. Pamenepo amene ali otsirizira adzakhala oyambirira, ndipo amene ali oyambirira adzakhala otsirizira.” Nthaŵi yomweyo Afarisi ena adadzauza Yesu kuti, “Muchokeko kuno, chifukwa Herode akufuna kukuphani.” Yesu adati, “Pitani kaiwuzeni nkhandweyo kuti ndikutulutsa mizimu yoipa ndiponso ndikuchiritsa anthu lero ndi maŵa, ndipo mkucha mpamene nditsirize ntchito yanga. Komabe ndiyenera kupitirira ndi ulendo wanga lero ndi maŵa ndi mkucha, pakuti mneneri sangafere kwina koma ku Yerusalemu. “Iwe Yerusalemu, Yerusalemu! Umapha aneneri nkuŵaponya miyala anthu amene Mulungu amakutumizira. Nkangati ndakhala ndikufuna kusonkhanitsa anthu ako, monga momwe nkhuku imasonkhanitsira anapiye ake pansi pa mapiko ake, iwe nkumakana. Ndithu nyumba yanu yaikuluyi idzasanduka bwinja. Ndipo ndikunenetsa kuti simudzandiwonanso konse mpaka mudzati, ‘Ngwodala amene alikudza m'dzina la Ambuye.’ ” Pa tsiku lina la Sabata Yesu adakadya kwa mkulu wina wa m'gulu la Afarisi, ndipo Afarisi anzake ankamupenyetsetsa. Pomwepo pamaso pake panali munthu wina wambulu. Yesu adafunsa akatswiri a Malamulo ndi Afarisi kuti, “Kodi Malamulo amalola kuchiritsa munthu pa tsiku la Sabata, kapena ai?” Koma iwo adangoti chete. Tsono Yesu adatenga munthuyo, ndipo atamchiritsa, adamuuza kuti azipita. Kenaka adaŵafunsa kuti, “Ndani mwa inu, bulu wake kapena ng'ombe yake itagwa m'chitsime pa tsiku la Sabata, sangaitulutse pa Sabata pomwepo?” Iwo adasoŵa poyankha. Yesu adaaona kuti anthu amene adaaitanidwa kudzadya nao ankadzisankhira malo aulemu. Tsono adaŵaphera fanizo, adati, “Wina akakuitana ku phwando la ukwati, usamakhala pa malo aulemu ai, chifukwa mwina kapena adaitananso wina waulemu kuposa iwe. Ndiye iye uja amene adaitana aŵiri nonsenu nkudzakuuza kuti, ‘Pepani, patsani aŵa maloŵa.’ Apo iweyo udzachita manyazi pokakhala pa malo otsika. Koma akakuitana, kakhale pa malo otsika, kuti amene adakuitana uja adzakuuze kuti, ‘Bwenzi langa, dzakhale pa malo aulemu pano.’ Apo udzalandira ulemu pamaso pa onse amene uli nao podyera. Pajatu aliyense wodzikuza adzamchepetsa, ndipo aliyense wodzichepetsa adzamkuza.” Yesu adauzanso Mfarisi uja amene adaamuitana kudzadya naye kuti, “Ukamakonza chakudya chamasana kapena chamadzulo, usamaitana abwenzi ako, kapena abale ako, kapena a fuko lako, kapena anzako achuma, chifukwa mwina iwonso adzakuitanako, motero udzalandiriratu mphotho yako. Koma iwe ukamakonza phwando, uziitana amphaŵi, otsimphina, opunduka ndi akhungu. Apo udzakhala wodala, chifukwa iwo alibe kanthu koti nkukubwezera. Mulungu ndiye adzakubwezera, pamene anthu olungama adzauka kwa akufa.” Munthu wina amene ankadya nao, atamva zimenezi, adauza Yesu kuti, “Ngwodala munthu amene adzadye nao mu Ufumu wa Mulungu.” Koma Yesu adamuphera fanizo, adati, “Munthu wina adaakonza phwando lalikulu, naitana anthu ambiri. Nthaŵi ya phwando itakwana adatuma wantchito wake kukauza oitanidwa aja kuti, ‘Bwerani, pakuti zonse zakonzeka.’ Koma onsewo mmodzimmodzi adayamba kupereka zifukwa zokanira. Woyamba adati, ‘Ndidagula munda, tsono ndikuyenera kupita kuti ndikauwone. Pepani sindibwera.’ Wina adati, ‘Ndidagula ng'ombe khumi zapagoli, ndiye ndikukaziyesa. Pepani sindibwera.’ Ndipo wina adati, ‘Ndangokwatira tsopano apa, choncho sinditha kubwera.’ Tsono wantchitoyo atabwerako adadzasimbira mbuye wake zonsezo. Apo mwini nyumbayo adapsa mtima, nauza wantchito wakeyo kuti, ‘Pita msanga ku miseu yaikulu ndi yaing'ono ya mumzinda muno ukapeze anthu osauka, otsimphina, akhungu ndi opunduka, ukabwere nawo kuno.’ Atabwerako wantchito uja adati, ‘Bwana, ndachita zija munandilamulazi, koma malo akalipobe.’ Apo mbuye uja adamuuza wantchitoyo kuti, ‘Pita ku miseu ndi ku njira za kunja kwa mudzi, ukaŵakakamize anthu kubwera kuno, kuti nyumba yanga idzaze. Kunena zoona, mwa anthu amene ndidaaŵaitana aja palibe ndi mmodzi yemwe amene adzalilaŵe phwando langali.’ ” Chikhamu cha anthu chinkatsagana ndi Yesu. Tsono Iye adatembenuka naŵauza kuti, “Aliyense wofuna kukhala wophunzira wanga, azikonda Ine koposa atate ake ndi amai ake, mkazi wake ndi ana ake, abale ake ndi alongo ake, ndiponso koposa ngakhale moyo wake womwe. Aliyense amene sasenza mtanda wake nkumanditsata, sangakhale wophunzira wanga. “Wina mwa inu akafuna kumanga nyumba yosanja, kodi suja amayamba wakhala pansi nkuŵerenga ndalama zofunika, kuti aone ngati ali nazo zokwanira kuitsiriza? Akapanda kutero, mwina adzaika maziko, nkulephera kuitsiriza. Apo anthu onse, poona zimenezi, adzayamba kumseka. Adzati, ‘Mkulu uyu adaayamba kumanga nyumba, koma adalephera kuitsiriza.’ “Chimodzimodzinso kodi ndi mfumu iti, popita ku nkhondo kukamenyana ndi mfumu ina, siiyamba yakhala pansi nkuganiza bwino? Imaganiziratu ngati ndi asilikali zikwi khumi ingathe kukamenyana ndi mfumu ina ija, imene ikubwera ndi asilikali zikwi makumi aŵiri. Tsono ngati siingathe, idzatuma nthumwi kukapempha mtendere, mfumu ina ija ikali kutali. “Chonchonso aliyense mwa inu amene sasiya zonse zimene ali nazo, sangakhale wophunzira wanga.” “Mchere ndi wabwino. Koma ngati mcherewo watha mphamvu, mphamvu zakezo nkuzibwezeranso nchiyani? Ulibenso ntchito ngakhale pa munda, kapena pa dzala. Amangoutaya basi. Amene ali ndi makutu akumva, amve!” Anthu onse okhometsa msonkho ndi Ayuda enanso onyozera Malamulo ankabwera kwa Yesu kudzamva mau ake. Tsono Afarisi ndi aphunzitsi a Malamulo adayamba kuŵinya nkumanena kuti, “Munthu uyu amalandira anthu ochimwa, nkumadya nawo pamodzi.” Tsono Yesu adaŵaphera fanizo ili, adati, “Ndani mwa inu ali ndi nkhosa 100, imodzi itatayikapo, sangasiye nkhosa zina zonse 99 zija ku busa, nkukafunafuna yotayikayo mpaka ataipeza? Ndipo ataipeza, amaisenza pamapewa pake mokondwa. Pofika kwao, amasonkhanitsa abwenzi ake ndi anzake oyandikana nawo, naŵauza kuti, ‘Mukondwere nane pamodzi, chifukwa ndaipeza nkhosa yanga idaatayika ija.’ ” Yesu adapitiriza mau kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti momwemonso Kumwamba kudzakhala chimwemwe chifukwa cha munthu mmodzi wochimwa amene watembenuka mtima, kuposa anthu olungama 99 amene alibe chifukwa chotembenukira mtima.” “Mwinanso mai amakhala ndi tindalama khumi, kamodzi nkutayika. Kodi suja amayatsa nyale nasesasesa m'nyumba nkufunafuna mosamala mpaka atakapeza? Atakapeza amasonkhanitsa abwenzi ake ndi anzake oyandikana nawo, naŵauza kuti, ‘Mukondwere nane pamodzi, chifukwa ndakapeza kandalama kanga kaja kadaatayikaka.’ ” Yesu popitiriza mau adati, “Ndikunenetsa kuti ndi m'menenso angelo a Mulungu amakondwerera munthu mmodzi wochimwa amene watembenuka mtima.” Yesu adatinso, “Munthu wina adaali ndi ana aamuna aŵiri. Wamng'ono adapempha bambo wake kuti, ‘Atate, bwanji mugaŵiretu tsopano chuma chanu, ine mundipatsiretu chigawo changa.’ Bamboyo adaŵagaŵiradi ana ake aja chuma chake. Patangopita masiku oŵerengeka wamng'ono uja adagulitsa chigawo chake chonse, nachoka kwaoko ndi ndalama zake kupita ku dziko lakutali. Kumeneko adamwaza chuma chakecho ndi mayendedwe oipa. Chitamthera chuma chake chonse, mudaloŵa njala yaikulu m'dziko limeneli, mwakuti iye yemwe adayamba kusauka. Pamenepo adapita kukakhala nao kwa nzika ina ya m'dzikomo. Nzikayo idamtuma ku busa kukaŵeta nkhumba zake. Mnyamata uja ankalakalaka kudya makoko amene nkhumba zinkadya, koma panalibe munthu wompatsako ngakhale makokowo. “Atakhalakhala adadzidzimuka mumtima mwake, ndipo adati, ‘Achulukirenji antchito a bambo wanga amene ali ndi chakudya chokwanira mpaka kutsalako, pamene ine kuno ndikufa ndi njala. Basi ndinyamuka, ndipita kwa bambo wanga, ndipo ndikanena kuti: Atate, ndidachimwira Mulungu wakumwamba, ndi inu nomwe. Sindili woyenera kutchedwanso mwana wanu. Mundilole ndisanduke mmodzi mwa antchito anu.’ “Choncho adanyamukadi napita kwa bambo wake. Koma akubwera patali, bambo wake adamuwona, namumvera chisoni. Adamthamangira, namkumbatira, nkumamumpsompsona. Mwanayo adati, ‘Atate, ndidachimwira Mulungu wakumwamba, ndi inu nomwe. Sindili woyenera kuchedwanso mwana wanu.’ Koma bambo wake adauza antchito ake kuti, ‘Thamangani mukatenge mkanjo wabwino kwambiri, mumuveke. Mumuvekenso mphete ku chala, ndi nsapato ku mapazi. Ndipo katengeni mwanawang'ombe wonenepa uja, muphe kuti tidye, tikondwere. Chifukwa mwana wangayu adaafa, koma tsopano wakhalanso moyo; adaatayika, koma tsopano wapezeka.’ Ndiye pompo chikondwerero chidayamba. “Koma mwana wake wamkulu uja anali ku munda. Pochokera kumundako, atafika pafupi ndi nyumba, adamva anthu akuimba ndi kuvina. Adaitana wantchito mmodzi namufunsa kuti, ‘Kodi kwagwanji?’ Iye adati, ‘Mng'ono wanu uja wabwera, ndiye bambo apha mwanawang'ombe wonenepa uja chifukwa amlandira ali wamoyo.’ Atamva zimenezo mwana wamkuluyo adapsa mtima, nakana kuloŵa. Apo bambo wake adatuluka, nkumupempha mopemba kuti aloŵe. Koma iye adayankha bambo akewo kuti, ‘Ine zaka zonsezi ndakhala ndikukugwirirani ntchito ndipo sindidalakwirepo lamulo lanu. Komabe inu simudandipatsepo ndi katonde komwe kuti ndikondwere pamodzi ndi anzanga. Koma mwana wanuyu, chuma chanu chonse adaonongera akazi achiwerewere, ndipo pamene wabwera, mwamuphera mwanawang'ombe wonenepa uja!’ “Bambo wakeyo adamuyankha kuti, ‘Mwana wanga, iwe uli ndi ine nthaŵi zonse, ndipo zanga zonse nzako. Kunayenera kuti tikondwere ndi kusangalala, chifukwa mng'ono wakoyu adaafa, koma tsopano wakhalanso moyo; adaatayika, koma tsopano wapezeka.’ ” Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Panali munthu wina wachuma amene anali ndi kapitao wake. Anthu adaadzamneneza kapitaoyo kuti akumwaza chuma cha mbuye wake. Tsono mbuye wakeyo adamuitana, namufunsa kuti, ‘Nchiyani chimene ndikumva za iwe? Undifotokozere za ukapitao wako, pakuti sungakhalenso kapitao ai.’ Apo kapitaoyo adayamba kuganiza mumtima mwake kuti, ‘Ndichite chiyani, popeza kuti mbuye wanga akundilanda ukapitao? Kulima, ai, ndilibe mphamvu. Kupemphapempha, ainso, kukundichititsa manyazi. Chabwino, tsopano ndadziŵa choti ndichite, kuti anthu akandilandire ku nyumba zao, ukapitao ukandithera.’ Motero adaitana angongole a mbuye wake mmodzimmodzi. Adafunsa woyamba kuti, ‘Kodi uli ndi ngongole yotani kwa mbuye wanga?’ Iye adati, ‘Mafuta amuyeso wokwanira mitsuko makumi khumi.’ Kapitaoyo adamuuza kuti, ‘Nayi kalata yako yangongole, khala pansi msanga, ungolembapo mitsuko makumi asanu.’ Adafunsanso wina kuti, ‘Nanga iwe, ngongole yako ndi yotani?’ Iye adati, ‘Tirigu wamuyeso wokwanira matumba makumi khumi.’ Kapitaoyo adamuuza kuti, ‘Nayi kalata yako yangongole, ungolembapo matumba makumi asanu ndi atatu.’ Apo mbuye wa kapitao wonyenga uja adamuyamikira chifukwa cha kuchenjera kwake. Pajatu pokhala ndi anzao, anthu ongokonda zapansipano ngochenjera koposa anthu okhala m'kuŵala kwa Mulungu.” Yesu popitiriza mau adati, “Ndipo Ine ndikukuuzani kuti mudzipezere abwenzi ndi chuma chonyengachi. Apo chumacho chikadzakutherani, Mulungu adzakulandirani ku nyumba zamuyaya. Wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ngwokhulupirikanso pa zazikulu. Ndipo wonyenga pa zazing'ono, amanyenganso pa zazikulu. Tsono ngati mwakhala osakhulupirika pa chuma chonyengachi, ndani nanga adzakusungizeni chuma chenicheni? Ndipo ngati mwakhala osakhulupirika ndi za wina, ndani adzakupatseni zimene zili zanuzanu? “Palibe wantchito amene angathe kutumikira mabwana aŵiri, pakuti kapena adzadana ndi mmodzi nkukonda winayo, kapena adzadzipereka kwa mmodzi nkunyoza winayo. Simungathe kutumikira onse aŵiri, Mulungu ndi chuma.” Afarisi atamva zonsezi, adamseka Yesu, chifukwa iwo anali okonda ndalama. Ndipo Iye adaŵauza kuti, “Inu mumadziwonetsa olungama pamaso pa anthu, koma Mulungu amaidziŵa mitima yanu. Pajatu zimene anthu amaziyesa zamtengowapatali, m'maso mwa Mulungu zimaoneka zonyansa. “Malamulo a Mose ndi zolemba za aneneri zinkagwirabe ntchito mpaka nthaŵi ya Yohane Mbatizi. Kuyambira pamenepo Uthenga Wabwino ukulalikidwa wakuti Mulungu akukhazikitsa ufumu wake, ndipo anthu onse akuyesetsa mwamphamvu kuloŵamo. Koma nkwapafupi kuti thambo ndi dziko lapansi zithe, kupambana kuti kalemba kakang'ono ka pa Malamulo kathe mphamvu. “Aliyense amene asudzula mkazi wake, nakwatira wina, akuchita chigololo. Ndipo amene akwatira mkazi wosudzulidwayo, nayenso akuchita chigololo.” “Panali munthu wina wachuma, amene ankavala zovala zamtengowapatali, ndipo ankasangalala ndi kudyerera masiku onse. Panalinso munthu wina, dzina lake Lazaro, amene ankadzagona pa khomo la munthu wachuma uja. Iyeyu anali ndi zilonda m'thupi lonse. Ankalakalaka kudya nyenyeswa zimene zinkagwa pansi kuchokera pa tebulo la wachuma uja. Koma si pokhapo, ngakhale agalu ankabwera kumadzanyambita zilonda zake. “Munthu wosauka uja adamwalira, angelo nkumunyamula, nakamtula m'manja mwa Abrahamu. Munthu wachuma uja nayenso adamwalira, naikidwa m'manda. Pamene ankazunzika ku Malo a anthu akufa, wachuma uja adayang'ana kumwamba naona Abrahamu ali patali, ndi Lazaro ali pambali pakepa. Pamenepo adanena mokweza mau kuti, ‘Atate Abrahamu, mundichitire chifundo. Tumani Lazaro aviike nsonga ya chala chake m'madzi kuti adzaziziritseko lilime langa, pakuti ndikuzunzika koopsa m'moto muno.’ Koma Abrahamu adati, ‘Mwana wanga, kumbukira kuti udalaandiriratu zokondweretsa ukadali ndi moyo, pamene Lazaro adaalandira zoŵaŵa. Koma tsopano iye akusangalala kuno, pamene iwe ukuzunzika kwambiri. Ndiponso pakati pa ife ndi inu pali chiphompho, kotero kuti ofuna kuchoka kuno kuwolokera kwanuko, sangathe ai. Chimodzimodzinso kuchoka kwanuko kuwolokera kuno.’ “Apo wachuma uja adati, ‘Ndipotu ndikukupemphani atate, kuti mumtume Lazaroyo apite ku nyumba ya bambo wanga. Kumeneko ndili ndi abale anga asanu. Akaŵachenjeze, kuwopa kuti iwonso angabwere ku malo ano amazunzo.’ Koma Abrahamu adati, ‘Iwo ali ndi mabuku a Mose ndi a aneneri. Amvere zam'menemo.’ Iye adati, ‘Iyai, atate Abrahamu, koma wina atauka kwa akufa nkupita kwa iwo, apo adzatembenuka mtima.’ Koma Abrahamu adamuuza kuti, ‘Ngatitu iwo samvera Mose ndi aneneri, sangathekenso ngakhale wina auke kwa akufa.’ ” Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Zochimwitsa anthu sizingalephere kuwoneka, koma tsoka kwa munthu wobwera nazoyo. Kukadakhala kwabwino kuti ammangirire chimwala cha mphero m'khosi ndi kukamponya m'nyanja, kupambana kuti achimwitse mmodzi mwa ana ang'onoang'onoŵa. Chenjerani tsono! “Mbale wako akachimwa, umdzudzule. Akatembenuka mtima, umkhululukire. Akakuchimwira kasanunkaŵiri pa tsiku, nabwera kasanunkaŵiri kudzanena kuti, ‘Pepani,’ umkhululukire ndithu.” Atumwi adapempha Ambuye kuti, “Mutiwonjezere chikhulupiriro.” Koma Ambuye adati, “Mukadakhala ndi chikhulupiriro ngakhale chochepa kwambiri ngati kambeu ka mpiru, bwenzi mutauza mkuyu uwu kuti, ‘Zuka, kadzibzale m'nyanja,’ ndipo ukadakumverani ndithu.” Yesu adatinso, “Utha kukhala ndi wantchito wolima ku munda kapena woŵeta nkhosa. Pamene iye wafika kuchokera ku munda, kodi ungamuuze kuti, ‘Bwera msanga, udzadye?’ Sungatero ai, koma udzamuuza kuti, ‘Konzere chakudya. Ukonzeke kunditumikira mpaka ineyo ndidye ndi kumwa. Iweyo udya ndi kumwa pambuyo pake.’ Kodi ungamthokoze wantchitoyo chifukwa chakuti wachita zimene unamlamula? Choncho inunso, mutachita zonse zimene adakulamulani, muziti, ‘Ndife antchito osayenera kulandira kanthu. Tangochita zimene tinayenera kuchita.’ ” Pa ulendo wake wopita ku Yerusalemu, Yesu adadzera m'malire a Samariya ndi Galileya. Pamene ankaloŵa m'mudzi wina, anthu khumi akhate adadzamchingamira. Adaima kutali, nanena mokweza mau kuti, “Yesu Ambuye, tichitireni chifundo.” Pamene Yesu adaŵaona, adaŵauza kuti, “Pitani, kadziwonetseni kwa ansembe.” Pamene iwo ankapita, adachira. Tsono mmodzi mwa iwo, ataona kuti wachira, adabwerera nayamba kuyamika Mulungu mokweza mau. Adagwada nkuŵerama kwambiri pamaso pa Yesu, namthokoza. Koma munthuyo anali Msamariya. Apo Yesu adati, “Kodi achira aja si khumi? Nanga asanu ndi anai ena aja ali kuti? Ndiye kuti sadabwerere wina aliyense kudzayamika Mulungu, koma mlendo yekhayu?” Kenaka Yesu adauza munthuyo kuti, “Nyamuka, pita. Chikhulupiriro chako chakuchiritsa.” Afarisi ena adafunsa Yesu kuti, “Kodi Mulungu adzakhazikitsa liti ufumu wake?” Yesu adaŵayankha kuti, “Mulungu sakhazikitsa ufumu wake mooneka ndi maso ai. Anthu sadzati, ‘Suuwu, uli pano,’ kapena, ‘Suuwo,’ pakuti ngakhale tsopano Mulungu akukhazikitsa ufumu wake pakati panu.” Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Akudza masiku pamene mudzalakalaka kuwona nthaŵi ya kudza kwa Mwana wa Munthu ngakhale tsiku limodzi lokha, koma simudzaloledwa ai. Anthu azidzakuuzani kuti, ‘Suuwo uli uko,’ kapena, ‘Suuwu uli pano,’ musadzapiteko kapena kuŵatsatira ai. Pajatu monga mphezi imang'anipa nkuŵala kuchokera mbali ina ya kuthambo kufikira mbali yake ina, Mwana wa Munthu adzateronso pa tsiku la kubwera kwake. Koma Iye ayenera kuti ayambe wamva zoŵaŵa zambiri, ndipo kuti anthu amakono amkane. “Monga momwe zidaachitikira pa nthaŵi ya Nowa, zidzateronso pa nthaŵi ya Mwana wa Munthu. Masiku amenewo anthu ankangodya ndi kumwa, ankakwatira ndi kumakwatiwa, mpaka tsiku limene Nowa adaloŵa m'chombo. Pamenepo chigumula chidafika nkuŵaononga onse. Monga momwe zidaachitikiranso pa nthaŵi ya Loti. Anthu ankangodya ndi kumwa, ankagulitsana malonda, ankabzala mbeu, ankamanga nyumba. Koma tsiku limene Loti adatuluka m'Sodomu, Mulungu adagwetsa moto ndi miyala yoyaka ya sulufule nkuŵaononga onsewo. Zidzateronso pa tsiku limene Mwana wa munthu adzaoneke. “Tsiku limenelo, amene ali pa denga, asadzatsike kukatenga katundu wake m'nyumba. Chimodzimodzinso amene ali ku munda, asadzabwerere ku nyumba. Kumbukirani za mkazi wa Loti. Aliyense woyesa kudzisungira moyo wake, adzautaya, koma woutaya adzausunga. Kunena zoona, usiku umenewo, padzakhala anthu aŵiri pa bedi limodzi, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya. Azimai aŵiri adzakhala akusinja pamodzi, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya, Anthu aŵiri adzakhala ali m'munda, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya.” Apo ophunzira ake adamufunsa kuti, “Kodi zimenezi zidzachitikira kuti, Ambuye?” Yesu adati, “Kumene kwafera chinthu, nkumeneko kumasonkhana miphamba.” Yesu adaŵaphera fanizo pofuna kuŵaphunzitsa kuti azipemphera nthaŵi zonse, osataya mtima. Adati, “M'mudzi mwina mudaali woweruza wina amene sankaopa Mulungu kapena kulabadako za munthu. M'mudzi momwemo mudaalinso mai wamasiye. Iyeyu ankabwera kwa woweruza uja kudzampempha kuti, ‘Mundiweruzireko mlandu umene uli pakati pa ine ndi mdani wanga.’ Kwa nthaŵi yaitali woweruza uja ankakana, koma pambuyo pake adaganiza kuti, ‘Ngakhale sindiwopa Mulungu kapena kusamala munthu, komabe chifukwa mai wamasiyeyu akundivuta, ndimuweruzira mlandu wake, kuwopa kuti angandilemetse nako kubwerabwera kwake.’ ” Tsono Ambuye adati, “Mwamvatu mau a woweruza wosalungama uja. Nanga Mulungu, angaleke kuŵaweruzira mlandu wao osankhidwa ake, amene amamdandaulira usana ndi usiku? Kodi adzangoŵalekerera? Iyai, kunena zoona adzaŵaweruzira mlandu wao msanga. Komabe Mwana wa Munthu pobwera, kodi adzapezadi chikhulupiriro pansi pano?” Yesu adaŵapheranso fanizo anthu ena amene ankadziyesa olungama nkumanyoza anzao. Adati, “Anthu aŵiri adaapita ku Nyumba ya Mulungu kukapemphera. Wina anali Mfarisi, wina anali wokhometsa msonkho. Mfarisiyo adaimirira nayamba kupemphera motere mumtima mwake: ‘Mulungu, ndikukuyamikani kuti ine sindili monga anthu ena onse ai. Iwowo ndi anthu akuba, osalungama ndi adama. Sindilinso monga wokhometsa msonkho uyu ai. Ine ndimasala zakudya kaŵiri pa mlungu, ndipo ndimapereka chachikhumi pa zonse zimene ndimapata.’ Koma wokhometsa msonkho uja adaima kutali, osafuna nkuyang'ana kumwamba komwe. Ankangodzigunda pa chifuwa ndi chisoni nkumanena kuti, ‘Mulungu, mundichitire chifundo ine wochimwane.’ ” Yesu popitiriza mau adati, “Kunena zoona, wokhometsa msonkhoyu adabwerera kwao ali wolungama pamaso pa Mulungu, osati Mfarisi uja ai. Pajatu aliyense wodzikuza adzamchepetsa, ndipo wodzichepetsa, adzamkuza.” Anthu ena ankabwera ndi ana omwe kwa Yesu kuti aŵakhudze. Ophunzira ake poona zimenezi, ankaŵazazira. Koma Yesu adaŵaitana nati, “Alekeni anaŵa azibwera kwa Ine, musaŵaletse. Paja Ufumu wa Mulungu ndi wa anthu otere. Ndithu ndikunenetsa kuti amene salandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana, ameneyo sadzaloŵamo.” Mkulu wina adafunsa Yesu kuti, “Aphunzitsi abwino, kodi ndizichita chiyani kuti ndikalandire moyo wosatha?” Yesu adamuyankha kuti, “Ukunditchuliranji wabwino? Wabwinotu ndi mmodzi yekha, Mulungu basi. Malamulo ukuŵadziŵa: Usachite chigololo, usaphe, usabe, usachite umboni wonama, lemekeza atate ako ndi amai ako.” Munthu uja adati, “Zonsezi ndakhala ndikuzitsata kuyambira ndili mwana.” Pamene Yesu adamva zimenezi, adamuuza kuti, “Ukusoŵabe chinthu chimodzi: kagulitse zonse zimene uli nazo. Ndalama zake ukapatse anthu osauka, ndipo chuma udzachipeza Kumwamba. Kenaka ubwere, uzidzanditsata.” Koma pamene munthu uja adamva zimenezi, adavutika mu mtima, pakuti adaali wolemera kwambiri. Yesu adamuyang'ana, nanena kuti, “Nkwapatali kwambiri kwa anthu achuma kuti akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu. Nkwapafupi kuti ngamira idzere pa kachiboo ka zingano, kupambana kuti munthu wolemera akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.” Anthu amene adamva zimenezi adafunsa kuti, “Tsono nanga angathe kupulumuka ndani?” Yesu adati, “Zimene zili zosatheka ndi anthu, zimatheka ndi Mulungu.” Pamenepo Petro adati, “Ifetu paja tidasiya zonse kuti tizikutsatani.” Yesu adaŵauza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti aliyense wosiya nyumba, kapena mkazi, kapena abale, kapena makolo, kapena ana chifukwa cha Ufumu wa Mulungu, ameneyo pansi pompano adzalandira zonsezo mochuluka kwambiri koposa kale, kenaka kutsogoloko adzalandira moyo wosatha.” Yesu adatengera ophunzira ake pambali, naŵauza kuti, “Tilitu pa ulendo wopita ku Yerusalemu, ndipo zonse zidzachitika zimene aneneri adalemba zokhudza Mwana wa Munthu. Akampereka kwa anthu akunja. Amenewo akamchita chipongwe, akamnyazitsa, ndi kumthira malovu. Akamkwapula, nkumupha, koma mkucha wake Iye adzauka.” Ophunzira aja sadamvetse konse zimenezi. Tanthauzo la mau ameneŵa linali lobisika kwa iwo, nchifukwa chake sadamvetsetse zimene Yesu ankanenazo. Pamene Yesu ankayandikira ku Yeriko, munthu wina wakhungu adaakhala pamphepete pa mseu akupemphapempha kwa anthu. Atamva anthu ambirimbiri akupita mumseumo, adafunsa kuti, “Kodi kuli chiyani?” Adamuyankha kuti, “Kukupita Yesu wa ku Nazarete.” Apo iye adanena mokweza mau kuti, “Inu Yesu, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!” Anthu amene anali patsogolo adamzazira, adati, “Khala chete!” Koma iye adafuulirafuulira kuti, “Inu Mwana wa Davide, chitireni chifundo!” Yesu adaima nalamula kuti abwere naye kwa Iye. Atafika pafupi, Yesu adamufunsa kuti, “Kodi ukufuna kuti ndikuchitire chiyani?” Iye adati, “Ambuye, ndikufuna kuti ndizipenyanso.” Yesu adamuuza kuti, “Penya. Chikhulupiriro chako chakuchiritsa.” Nthaŵi yomweyo adapenyanso nayamba kutsata Yesu, akuthokoza Mulungu. Anthu onse aja ataona zimenezi, adatamanda Mulungu. Yesu adaloŵa m'Yeriko, ulendo wake wobzola mzindawo. Kudafika munthu wina, dzina lake Zakeyo. Iyeyo anali mkulu wa okhometsa msonkho, ndipo anali wolemera. Ankafunitsitsa kuwona Yesu kuti ngwotani. Koma pakuti Zakeyoyo anali wamfupi, adalephera kumuwona chifukwa cha kuchuluka kwa anthu. Tsono adathamangira kutsogolo, nakakwera mu mkuyu kuti amuwone, chifukwa Yesu ankayenera kudzera pamenepo. Ndiye pamene Yesu adafika pamalopo, adayang'ana m'mwamba, namuuza kuti, “Zakeyo, fulumira, tsika, chifukwa lero ndikuyenera kukakhala nao kunyumba kwako.” Pompo Zakeyo adafulumira, natsika, kenaka nkukamlandiradi Yesu mokondwa kwambiri. Poona zimenezi, anthu onse adayamba kung'ung'udza. Adati, “Wakakhala kunyumba kwa munthu wochimwa.” Koma Zakeyo adaimirira nauza Ambuye kuti, “Ambuye, ndithudi ndidzapereka hafu la chuma changa kwa amphaŵi. Ndipo ngati ndidalandira kanthu kwa munthu aliyense monyenga, ndidzamubwezera kanai.” Apo Yesu adamuuza kuti, “Chipulumutso chafika m'banja lino lero, popeza kuti ameneyunso ndi mwana wa Abrahamu. Pajatu Mwana wa Munthu adabwera kudzafunafuna ndi kudzapulumutsa amene adatayika.” Anthu ankamva zimene Yesu ankalankhula. Tsono adaŵaphera fanizo, popeza kuti anali pafupi ndi Yerusalemu, ndipo anthuwo ankaganiza kuti Mulungu akhazikitsa ufumu wake posachedwa. Adati, “Munthu wina, wa fuko lomveka, adapita ku dziko lakutali kukalandira ufumu kuti pambuyo pake abwerenso kwao. Adaitana khumi mwa antchito ake naŵapatsa ndalama zasiliva khumi, aliyense yakeyake. Adaŵauza kuti, ‘Bachita nazoni malonda mpaka nditabwera.’ Koma anthu ake ankadana naye, choncho m'mbuyo muno adatuma nthumwi kuti zipite ku dziko lomwelo nkukanena kuti, ‘Ife sitikufuna konse kuti munthu ameneyu akhale mfumu yathu.’ “Komabe iye adalandira ufumu uja. Tsono atabwerera kwao, adaitanitsa antchito aja adaaŵapatsa ndalamaŵa kuti adziŵe zimene adapindula. Woyamba adadza nati, ‘Ambuye, ndalama yanu ija idapindula ndalama makumi khumi.’ Mbuye wake adamuuza kuti, ‘Udachita bwino, ndiwe mtumiki wabwino. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zochepa kwambiri, udzalamulira midzi khumi.’ Wachiŵiri adadza nati, ‘Ambuye, ndalama yanu ija idapindula ndalama makumi asanu.’ Iyenso mbuye wake adamuuza kuti, ‘Iwe udzalamulira midzi isanu.’ Koma wina adadza nati, ‘Ambuye, nayi ndalama yanu ija. Ndidaaimanga pa kansalu. Ndinkakuwopani, popeza kuti ndinu munthu wankhwidzi. Mumalonjerera zimene simudaikize, ndiponso mumakolola zimene simudabzale.’ Apo mbuye wake uja adamuuza kuti, ‘Ndiwe wantchito woipa, ndikutsutsa ndi mau ako omwe. Kani unkadziŵa kuti ndine munthu wankhwidzi, amene ndimalonjerera zimene sindidaikize, ndipo ndimakolola zimene sindidabzale. Nanga bwanji osaiika ku banki ndalama yangayo, kuti ine pobwera ndiilandire pamodzi ndi chiwongoladzanja chake?’ Atatero adauza anthu amene anali pomwepo kuti, ‘Mlandeni ndalamayi muipereke kwa amene ali ndi ndalama makumi khumiyo.’ “Iwo adamuyankha kuti, ‘Pepani, ambuye, ameneyu ali kale ndi ndalama makumi khumi.’ Koma iye adati, ‘Ndikunenetsa kuti aliyense amene ali ndi kanthu, adzamuwonjezera zina. Koma amene alibe, ngakhale kamene ali nakoko adzamlandabe. Koma adani angaŵa, aja ankakana kuti ndikhale mfumu yaoŵa, bwera nawoni kuno, muŵaphe ine ndikuwona.’ ” Yesu atanena zimenezi, adatsogolera ophunzira ake kupita ku Yerusalemu. Atafika pafupi ndi midzi ya Betefage ndi Betaniya, pafupi ndi phiri lotchedwa Phiri la Olivi, adatuma ophunzira aŵiri, naŵauza kuti, “Pitani m'mudzi mukuwonawo. Mukakangoloŵamo mukapeza mwanawabulu ali chimangire, amene munthu sanakwerepo chikhalire. Mukammasule, nkubwera naye kuno. Wina akakakufunsani kuti, ‘Mukummasuliranji?’ Mukati, ‘Ambuye ali naye ntchito.’ ” Aŵiriwo adapita, nakapezadi monga momwe Yesu adaaŵauzira. Pamene ankamasula mwanawabuluyo, eniake adaŵafunsa kuti, “Mukummasuliranji mwanawabuluyu?” Iwo adati, “Ambuye ali naye ntchito.” Tsono adapita naye kwa Yesu, nayamba kuyala zovala zao pa buluyo, nakwezapo Yesu. Pamene Yesu ankapita, anthu adamchitira ulemu pakuyala zovala zao mu mseu. Pamene ankayandikira Yerusalemu, pa matsitso a Phiri la Olivi, gulu lonse la omutsatira aja lidayamba kukondwerera. Adakweza mau, natamanda Mulungu chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu zimene iwo adaziwona. Adati, “Ndi yodala Mfumu imene ilikudza m'dzina la Ambuye. Mtendere Kumwamba, ulemu kwa Mulungu kumwambamwamba.” Apo Afarisi ena amene adaali m'khamumo adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, auzeni ophunzira anuŵa aleke zimenezi.” Iye adati, “Ndikutitu iwoŵa akangokhala chete, ifuula ndi miyalayi.” Yesu atayandikira, nkuwona Yerusalemu, adalira chifukwa cha mzindawo. Adati, “Ha, iwenso ukadangodziŵa lero lino zinthu zopatsa mtendere! Koma ai, tsopano maso ako sangathe kuziwona. Nthaŵi idzakufikira pamene adani ako adzakuzinga ndi machemba, nadzakuzungulira, nkukutsekereza ponseponse. Adzakusakaziratu iweyo pamodzi ndi anthu ako onse. Sadzasiya mwa iwe mwala pamwamba pa unzake, chifukwa chakuti sudazindikire nthaŵi imene Mulungu adaati adzakupulumutse.” Yesu adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, nayamba kutulutsa anthu amene ankachita malonda m'menemo. Adaŵauza kuti, “Malembo akuti, ‘Nyumba yanga idzakhala nyumba yopemphereramo.’ Koma inu mwaisandutsa phanga la achifwamba.” Yesu ankaphunzitsa m'Nyumba ya Mulungu tsiku ndi tsiku. Akulu a ansembe, aphunzitsi a Malamulo ndiponso akulu a Ayuda ankafuna kumupha, koma adaasoŵa chochita, chifukwa anthu onse ankatengeka nawo mtima mau ake. Tsiku lina Yesu ankaphunzitsa anthu m'Nyumba ya Mulungu nkumalalika Uthenga Wabwino. Tsono akulu a ansembe, aphunzitsi a Malamulo ndiponso akulu a Ayuda adabwera namufunsa kuti, “Mutiwuze, kodi mphamvu zoti muzichita zimenezi mudazitenga kuti? Kaya ndani adakupatsani mphamvu zimenezi?” Yesu adati, “Nanenso ntakufunsani funso limodzi. Tandiwuzani, kodi Yohane Mbatizi kuti azibatiza, mphamvu zake adaazitenga kwa yani, kwa Mulungu kapena kwa anthu?” Iwo aja adayamba kukambirana nkumati, “Tikati adaazitenga kwa Mulungu, Iyeyu anena kuti, ‘Nanga bwanji tsono sumudamkhulupirire?’ Komanso tikati adaazitenga kwa anthu, anthu onseŵa atiponya miyala, chifukwa mumtima mwao amatsimikiza kuti Yohane adaali mneneri.” Ndiye adangomuyankha kuti, “Kaya, ife sitikudziŵa kumene adaazitenga.” Apo Yesu adati, “Nanenso tsono sindikuuzani kumene ndidazitenga mphamvu zoti ndizichita zimenezi.” Pamenepo Yesu adaphera anthu aja fanizo lina. Adati, “Munthu wina adaalima munda wamphesa. Adaubwereka alimi, iye nkunyamuka ulendo wa ku dziko lina, nakakhalako nthaŵi yaitali. Nyengo yothyola zipatso itafika, munthu uja adatuma wantchito wake kwa alimi aja, kuti akampatsireko zipatso za m'munda muja. Koma alimiwo adammenya, nkumubweza osampatsa kanthu. Adatumanso wantchito wina. Nayenso alimi aja adammenya, namchita chipongwe, nkumubweza osampatsa kanthu. Adatumanso wachitatu, koma uyunso alimiwo adamuvulaza, namtaya kunja. Pambuyo pake mwini munda uja adati, ‘Ndichite chiyani tsopano? Ndidzatuma mwana wanga amene ndimamkonda uja. Mwina mwake iye yekhayu akamchitira ulemu.’ Koma alimi aja atamuwona, adayamba kuuzana kuti, ‘Uyu ndiye amene adzamsiyire chumachi. Tiyeni timuphe kuti chidzakhale chathu.’ Tsono adamuponya kunja kwa mundawo, namupha. Kodi mwini munda wamphesa uja adzaŵatani alimi aja? Ndithu adzabwera naŵapha alimiwo, munda uja nkuubwereka ena.” Anthu aja atamva zimenezi adati, “Ai, msatero.” Koma Yesu adaŵayang'ana nati, “Nanga tsono tanthauzo lake nchiyani Malembo aŵa akuti, “ ‘Mwala umene amisiri omanga nyumba adaaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya, wofunika koposa?’ Aliyense wogwera pa mwala umenewo adzathyokathyoka. Ndipo aliyense amene mwalawo udzamugwere, udzangomutswanyiratu.” Aphunzitsi a Malamulo ndi akulu a ansembe adaadziŵa kuti fanizolo Yesu ankaphera iwowo. Nchifukwa chake ankafuna kumugwira nthaŵi yomweyo, koma ankaopa anthu. Tsono iwo ankangomuŵenda, choncho adatuma anthu omuzonda, odziwonetsa ngati anthu olungama, kuti akamutape m'kamwa. Ankafuna kukamneneza kwa bwanamkubwa, pakuti iyeyo ndiye anali ndi mphamvu ndi ulamuliro wonse. Ozondawo adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, tikudziŵa kuti Inu mumalankhula ndi kuphunzitsa molungama, simuyang'anira kuti uyu ndani. Mumaphunzitsa malamulo a Mulungu moona. Kodi Malamulo a Mulungu amatilola kuti tizikhoma msonkho kwa Mfumu ya ku Roma, kapena ai?” Koma Yesu podziŵa maganizo ao andale adati, “Tandiwonetsani ndalama. Kodi ili ndi nkhope ya yani, ndipo ili ndi dzina la yani?” Iwo aja adati, “Zonse ndi za Mfumu ya ku Roma.” Apo Yesu adaŵauza kuti, “Tsono perekani kwa Mfumu zake za Mfumu, ndiponso kwa Mulungu zake za Mulungu.” Choncho adalephera kumutapa m'kamwa pamaso pa anthu pa zimene Iye adalankhula. Iwo adathedwa nzeru ndi zimene Yesu adaayankha, nkungoti chete. Asaduki ena adadza kwa Yesu. Paja iwo amati akufa sadzauka. Adamufunsa Yesu kuti, “Aphunzitsi, Mose adatilembera lamulo lakuti, ‘Ngati munthu amwalira, nasiya mkazi wake, koma opanda ana, mbale wake wa womwalirayo aloŵe chokolo, kuti amuberekere ana mbale wake uja.’ Tsono padaali anthu asanu ndi aŵiri pachibale pao. Woyamba adaakwatira mkazi, koma adamwalira osamsiyira mwana. Chimodzimodzinso wachiŵiri, ndipo wachitatu nayenso adaloŵa chokolo. Onse aja asanu ndi aŵiri adachita chimodzimodzi, koma onse adamwalira osamsiyira ana mkaziyo. Potsiriza pake mai uja nayenso adamwalira. Nanga tsono pa tsiku lodzauka akufa, mwini mkaziyo adzakhala utiwuti, popeza kuti abale asanu ndi aŵiri onse aja adaamkwatirapo?” Yesu adaŵayankha kuti, “Anthu okhala pansi pano amakwatira ndi kukwatiwa. Koma amene amaŵayesa oyenera kukakhala ndi moyo kutsogoloko, anthu atauka kwa akufa, sadzakwatiranso kapena kukwatiwa ai. Iwo adzakhala ngati angelo, mwakuti sangafenso ai. Iwo ndi ana a Mulungu popeza kuti Iye adaŵaukitsa kwa akufa. Koma zakuti anthu adzauka kwa akufa, Mose yemwe adaanenapo kale. Paja pa mbiri ija ya chitsamba choyaka moto, iye akuŵatchula Ambuye kuti, ‘Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, Mulungu wa Yakobe.’ Ndiye kutitu sali Mulungu wa anthu akufa ai, koma wa anthu amoyo, chifukwa kwa Iye anthu onsewo ndi amoyo.” Apo ena mwa aphunzitsi a Malamulo adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, mwanena bwino.” Adaatero popeza kuti Asaduki aja sadalimbenso mtima kuti amufunse mafunso ena. Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi inu, bwanji amati Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndi mwana wa Davide? Paja Davide yemwe m'buku la Masalimo akuti, “ ‘Chauta adauza Mbuye wanga kuti: Khala ku dzanja langa lamanja mpaka nditasandutsa adani ako kuti akhale ngati chopondapo mapazi ako.’ “Davide akutchula Mpulumutsi wolonjezedwa uja kuti Mbuye wake. Tsono angakhale mwana wakenso bwanji?” Pamene anthu onse ankamvetsera zimene Yesu ankalankhula, Iye adauza ophunzira ake kuti, “Chenjera nawoni aphunzitsi a Malamulo. Amakonda kuyenda atavala mikanjo yaitali, ndi kuti anthu aziŵalonjera mwaulemu pa misika. Amakonda mipando yaulemu kwambiri m'nyumba zamapemphero ndiponso malo olemekezeka pa maphwando. Koma amaŵadyera chuma chao azimai amasiye, nkumapemphera mapemphero ataliatali monyengezera. Anthu ameneŵa adzalangidwa koposa.” Yesu atakweza maso, adaona anthu olemera akuponya zopereka zao m'bokosi la ndalama m'Nyumba ya Mulungu. Adaonanso mai wina wamasiye akuponyamo tindalama tiŵiri. Pamenepo Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti mai wamasiye wosaukayu waponyamo koposa ena onseŵa. Chifukwa ena onseŵa angoponyamo zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo. Koma maiyu, mwa umphaŵi wake, waponyamo zonse zimene anali nazo, ngakhale zimene akadagulira chakudya.” Anthu ena ankalankhula za Nyumba ya Mulungu kuti adaikongoletsa ndi miyala yokoma, ndiponso ndi mitulo yopereka kwa Mulungu. Yesu adati, “Kunena za zinthu mukuziwonazi, masiku adzabwera mwakuti sipadzatsala konse mwala ndi umodzi womwe pamwamba pa mwala unzake: yonse adzaigumula.” Anthu aja adafunsa Yesu kuti, “Aphunzitsi, zimenezi zidzachitika liti? Tidzaonera chiyani kuti zonsezi zili pafupi kuchitika?” Yesu adati, “Chenjerani kuti anthu angakusokezeni. Chifukwa kudzafika anthu ambiri m'dzina langa namadzanena kuti, ‘Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndine.’ Azidzatinso, ‘Nthaŵi yayandikira.’ Amenewo musadzaŵatsate. Ndipo pamene mudzamva za nkhondo ndi za zipoloŵe, musadzachite mantha. Zimenezi zidzayenera kuyamba zaoneka, koma sindiye kuti chimalizo chifika nthaŵi yomweyo.” Yesu adaŵauzanso kuti, “Mitundu yosiyanasiyana idzaukirana, maiko osiyanasiyana adzamenyana nkhondo. Kudzachita zivomezi zazikulu. Kudzakhala njala ndi mliri ku malo osiyanasiyana. Kudzakhalanso zoopsa ndi zizindikiro zodabwitsa mu mlengalenga. “Koma zisanachitike zonsezi, adzakugwirani ndi kukuzunzani. Adzapita nanu ku milandu ku nyumba zamapemphero, nadzakuponyani m'ndende. Adzakuperekani kwa mafumu ndi kwa akulu ena a Boma chifukwa chotsatira Ine. Umenewu udzakhala mpata wanu wondichitira umboni. Tsono mudziŵiretu kuti musadzachite kukonzekera mau oti mudzaŵayankhe pamlandupo. Ineyo ndidzakupatsani mau ndi nzeru zimene adani anuwo sadzatha konse kuzikana kapena kuzitsutsa. Makolo anu omwe, abale anu, anansi anu, ndi abwenzi anu, amenewo adzakuperekani kwa adani anu, ndipo ena mwa inu mudzaphedwa. Anthu onse adzadana nanu chifukwa cha Ine. Koma silidzatayikapo tsitsi lanu ndi limodzi lomwe. Mukadzalimbikira, ndiye mudzapate moyo wanu.” “Pamene mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, dziŵani kuti chiwonongeko chake chafika. Pamenepo amene ali m'Yudeya athaŵire ku mapiri, amene ali mumzinda atulukemo, ndipo amene ali ku minda asadzaloŵenso mumzindamo. Chifukwa masiku amenewo adzakhala masiku akulipsira, kuti zonse zija zimene zidaalembedwa m'Malembo zipherezere. Ali ndi tsoka azimai amene adzakhale ndi pathupi, ndiponso azimai oyamwitsa ana masiku amenewo. Pakuti padzagwa masautso aakulu pa dziko lino, ndipo Mulungu adzaŵakwiyira Aisraeleŵa. Adzaphedwa pa nkhondo yoopsa, nkutengedwa ngati akapolo a anthu a mitundu ina. Kenaka Yerusalemu akunja adzampondereza mpaka pa mapeto ake a nthaŵi ya akunjawo.” Dan. 9.26; Mika 3.12; Zak. 11.6. “Padzakhala zizindikiro zodabwitsa pa dzuŵa, pa mwezi ndi pa nyenyezi. Pansi pano anthu a mitundu yonse adzada nkhaŵa nkutha nzeru, pomva kukokoma kwa nyanja ndi mafunde ake. Ena adzakomoka ndi mantha poyembekezera zimene zikudza pa dziko lonse lapansi, pakuti mphamvu zonse zakuthambo zidzagwedezeka. Pamenepo anthu adzaona Mwana wa Munthu akubwera pa mitambo, ali ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu. Zimenezi zikadzayamba kuchitika, mudzaimirire nkukweza mitu yanu, chifukwa chipulumutso chanu chayandikira.” Pambuyo pake Yesu adaŵaphera fanizo adati, “Yang'anani mkuyu ndi mitengo ina yonse. Mukamaona kuti masamba akuphuka, mumadziŵa kuti chilimwe chayandikira kale. Momwemonso, mukadzaona zija ndanenazi zikuchitika, mudzadziŵe kuti ufumu wa Mulungu uli pafupi. Ndithu ndikunenetsa kuti zonsezi zidzaoneka anthu a mbadwo unoŵa asanamwalire onse. Thambo ndi dziko lapansi zidzatha, koma mau anga sadzatha mphamvu konse.” “Chenjerani kuti mitima yanu ingapusitsidwe ndi maphwando, kuledzera, ndi kudera nkhaŵa za moyo uno, kuti tsikulo lingakufikireni modzidzimutsa. Pajatu lidzaŵagwera ngati msampha anthu onse okhala pa dziko lonse lapansi. Muzikhala maso tsono, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse, kuti mukhale ndi mphamvu zopulumukira ku zonsezi zimene ziti zidzachitike, ndiponso kuti mukaimirire pamaso pa Mwana wa Munthu.” Masiku onse Yesu ankaphunzitsa m'Nyumba ya Mulungu, koma usiku ankatuluka kukakhala ku phiri lotchedwa Phiri la Olivi. Tsono anthu onse ankalaŵirira m'mamaŵa kubwera kwa Iye ku Nyumba ya Mulungu kudzamva mau ake. Nthaŵi yochitira chikondwerero cha buledi wosafufumitsa inkayandikira. Chikondwererocho chimatchedwa Paska. Akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo ankafunafuna njira yoti aphere Yesu. Paja iwo ankaopa anthu. Tsono Satana adamuloŵa Yudasi wotchedwa Iskariote, amene anali mmodzi mwa ophunzira khumi ndi aŵiri aja a Yesu. Yudasiyo adapita kukapangana ndi akulu a ansembe ndi atsogoleri a alonda a ku Nyumba ya Mulungu za njira yoti aperekere Yesu kwa iwo. Iwo adakondwa, nalonjeza kumpatsa ndalama. Yudasi adavomera, nayamba kufunafuna mpata woti amuperekere kwa iwo, anthu onse osadziŵa. Tsiku la buledi wosafufumitsa lidafika, ndiye kuti tsiku limene anthu ankapha mwanawankhosa wochitira phwando la Paska. Yesu adatuma Petro ndi Yohane naŵauza kuti, “Pitani mukatikonzere phwando la Paska kuti tikadye.” Koma iwo adamufunsa kuti, “Kodi tikakonzere kuti?” Yesu adati, “Mvetsani! Mukangoloŵa m'mudzimu, mukumana ndi munthu wamwamuna atasenza mtsuko wa madzi. Mukamtsatire mpaka kunyumba kumene akaloŵe. Mukauze mwini nyumbayo kuti, ‘Aphunzitsi akufunsa kuti, kodi nchiti chipinda chimene Iwowo adzadyeremo phwando la Paska ndi ophunzira ao?’ Iyeyo akakuwonetsani chipinda chachikulu cham'mwamba, momwe akonzamo zonse zofunikira. M'menemo mukatikonzere chakudya.” Tsono iwo adapita nakachipezadi monga momwe adaaŵauzira, ndipo adakonza phwando la Paska. Nthaŵi itakwana, Yesu adakakhala podyera pamodzi ndi atumwi ake aja. Tsono adaŵauza kuti, “Ndafunitsitsa kudya phwando ili la Paska pamodzi ndi inu ndisanayambe kumva zoŵaŵa. Pakuti kunena zoona, sindidzadyanso konse Paska, mpaka Paskayi itadzafika pake penipeni mu Ufumu wa Mulungu.” Atatero Yesu adatenga chikho, ndipo atathokoza Mulungu, adati, “Kwayani, imwani nonsenu. Ndithu ndikunenetsa kuti kuyambira tsopano sindidzamwanso konse chakumwa cha mtengo wamphesa, mpaka Mulungu atadzakhazikitsa ufumu wake.” Kenaka Yesu adatenga mkate, nathokoza Mulungu, nkuunyemanyema, nagawira ophunzira aja, ndipo adati, “Ili ndi thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi kuti muzindikumbukira.” Atatha kudya, adaŵapatsanso chikho, nati, “Chikhochi ndi chipangano chatsopano chimene magazi anga, omwe akukhetsedwa chifukwa cha inu, akuchitsimikizira. “Koma ndithudi wondipereka kwa adani akudya nane pamodzi pompano. Mwana wa Munthu akukaphedwadi, monga momwe Mulungu adazikonzeratu kale. Komabe ali ndi tsoka munthu amene akukapereka Mwana wa Munthuyo.” Apo onse adayamba kumafunsana kuti, “Kodi ndani mwa ife angachite zotere?” Tsono ophunzira aja adayamba kutsutsana kuti, “Kodi mwa ife amati wamkulu ndani?” Yesu adaŵauza kuti, “Pakati pa anthu akunja, mafumu amadyera anthu ao masuku pa mutu, ndipo amene amaŵaonetsa mphamvu zao, amatchedwa mfulu zopatsa.” Koma pakati pa inu zisamatero ai. Kwenikweni wamkulu mwa inu azikhala ngati wamng'ono mwa onse, ndipo mtsogoleri azikhala ngati wotumikira. Kodi wamkulu ndani? Ndi amene alikudya, kapena amene akumtumikira? Si amene alikudyayo nanga? Koma Ine ndili pakati panu ngati wotumukira. “Inu ndinu amene mwakhala ndi Ine pa masautso anga onse. Nchifukwa chake, monga Atate anga adandipatsa ufumu, Inenso ndikukupatsani ufumu. Ndikadzaloŵa mu ufumu wanga, muzidzadya ndi kumwa pamodzi nane, ndipo mudzakhala pa mipando yachifumu nkumaweruza mafuko khumi ndi aŵiri a Israele.” “Simoni, Simoni, chenjera! Mulungu walola Satana kuti akupeteni nonse ngati tirigu. Koma Ine ndakupempherera, kuti usaleke kundikhulupirira. Ndipo iweyo utatembenuka mtima, ukaŵalimbitse abale akoŵa.” Apo Petro adati, “Ambuye, ndili wokonzeka kupita nanu ku ndende, ngakhale kufa kumene.” Koma Yesu adamuyankha kuti, “Ndikukuuza, iwe Petro, kuti lero lomwe lino, tambala asanalire, ukhala utandikana katatu kuti Ine sundidziŵa.” Yesu adaŵafunsa kuti, “Nthaŵi ina ndidaakutumani opanda thumba la ndalama, kapena thumba lapaulendo, kapenanso nsapato. Kodi pamene paja mudaasoŵapo kanthu?” Iwo adati, “Iyai.” Yesu adaŵauza kuti, “Koma tsopano amene ali ndi thumba la ndalama, asalisiye. Chimodzimodzinso thumba lake lapaulendo. Ndipo amene alibe lupanga, agulitse mwinjiro wake nkugula lupanga. Ndithu ndikunenetsa kuti ziyenera kuchitikadi mwa Ine zimene Malembo adanena kuti, ‘Ankamuyesa mmodzi mwa anthu ophwanya malamulo.’ Ndipo zonse zimene zidalembedwa za Ine zikuchitikadi.” Ophunzirawo adati, “Ambuye, aŵa malupanga, tili nawo kale aŵiri.” Yesu adaŵauza kuti, “Chabwino, basi.” Pambuyo pake Yesu adatuluka mu mzinda napita ku Phiri la Olivi monga adaazoloŵera. Ndipo ophunzira ake adapita naye. Pamene adafika kumeneko, Yesu adaŵauza kuti, “Pempherani, kuti mungagwe m'zokuyesani.” Tsono adapatukana nawo kadera, kutalika kwake ngati pamene mwala ungafike munthu atauponya. Apo adagwada pansi nayamba kupemphera. Adati, “Atate, ngati mukufuna, mundichotsere chikho chamasautsochi. Komabe muchite zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.” [Pamenepo mngelo wochokera Kumwamba adamuwonekera namlimbitsa mtima. Koma Yesu adavutikabe koopsa mu mtima, nkumapemphera kolimba kuposa kale. Ndipo thukuta limene ankadza linali ngati madontho akuluakulu a magazi ogwera pansi.] Atapemphera, adaimirira napita kwa ophunzira ake. Adaŵapeza ali m'tulo chifukwa cha chisoni, ndipo adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukugona? Dzukani ndi kumapemphera, kuti mungagwe m'zokuyesani.” Yesu akulankhula choncho, padabwera khamu la anthu. Amene ankaŵatsogolera anali Yudasi, mmodzi mwa ophunzira khumi ndi aŵiri aja. Iyeyu adadza pafupi ndi Yesu kuti amumpsompsone. Koma Yesu adamufunsa kuti, “Yudasi, mongadi ukupereka Mwana wa Munthu kwa adani pakumumpsompsona?” Ophunzira amene anali pafupi ndi Yesu ataona zimene zinalikudzachitika, adafunsa Yesu kuti, “Ambuye, kodi tiŵateme ndi lupanga?” Apo mmodzi mwa iwo adatemadi wantchito wa mkulu wa ansembe onse, mpaka kumusenga khutu la ku dzanja lamanja. Koma Yesu adati, “Basi, lekani zimenezi.” Atatero adakhudza khutu la munthuyo namchiritsa. Kenaka Yesu adalankhula nawo onse amene adaabwera kudzamugwira, akulu a ansembe ndi atsogoleri a alonda a ku Nyumba ya Mulungu, ndiponso akulu a Ayuda. Adaŵafunsa kuti, “Bwanji mwachita kunditengera malupanga ndi zibonga ngati kuti ndine chigaŵenga? Tsiku ndi tsiku ndidaali nanu m'Nyumba ya Mulungu, inuyo osandigwira. Koma ino ndi nthaŵi yanu ndiponso ya mphamvu za mdima.” Anthu aja adamugwira Yesu, napita naye ku nyumba ya mkulu wa ansembe onse. Petro ankaŵatsatira chapatali. Iwo adasonkha moto m'kati mwa bwalo la nyumbayo, nakhala pansi pamodzi. Petro nayenso adakakhala pakati pao. Mtsikana wina wantchito adamuwona atakhala nao pamotopo. Adamuyang'anitsitsa, nati, “Aŵansotu anali naye.” Koma Petro adakana, adati, “Mai iwe, sindimdziŵa ameneyu.” Patapita kanthaŵi pang'ono, munthu wina pomuwona adati, “Akulu inu, ndinunso mmodzi mwa iwo aja.” Koma Petro adati, “Munthu iwe, ai ndithu sindine.” Patapita ngati ora limodzi, munthu winanso adanenetsa kuti, “Ndithudi akulu aŵanso anali naye, pakuti ndi a ku Galileya.” Koma Petro adati, “Munthu iwe, sindikuzidziŵa zimene ukunenazi.” Ndipo pompo, akulankhulabe, tambala adalira. Ambuye adacheuka nayang'ana Petro. Pamenepo Petro adakumbukira mau aja amene Ambuye adaamuuza kuti, “Lero lomwe lino, tambala asanalire, ukhala utandikana katatu.” Pamenepo adatuluka, nakalira kwambiri chifukwa cha chisoni chachikulu. Tsono anthu amene ankalonda Yesu aja adayamba kumseka ndi kumammenya. Adammanga nsalu m'maso nkumamufunsa kuti, “Lota, wakumenya ndani?” Ndipo adamnenanso mau ena ambiri achipongwe. Kutacha, a m'Bungwe Lalikulu la Ayuda adasonkhana, ndiye kuti akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo. Adatenga Yesu napita naye ku Bwalo lao. Adamuuza kuti, “Ngati ndiwe Mpulumutsi wolonjezedwa uja, utiwuze mosabisa.” Koma Iye adaŵayankha kuti, “Ngakhale ntakuuzani, simungandikhulupirire konse, ndipo nditakufunsani funso, inu simungaliyankhe. Koma kuyambira tsopano Mwana wa Munthune ndidzakhala ku dzanja lamanja la Mulungu wamphamvuzonse.” Apo onse aja adati, “Tsono ndiye kutitu ndiwe Mwana wa Mulungu, ati?” Yesu adati, “Mwanena nokha kuti ndine amene.” Pamenepo iwo aja adati, “Tikufuniranji umboni wina? Tadzimvera tokha mau akeŵa.” Gulu lonse lija lidanyamuka nkupita naye Yesu kwa Pilato. Iwo adayamba kuneneza Yesu kuti, “Munthu uyu tidampeza akusokeza anthu a mtundu wathu. Amatiletsa kuti tisamakhome msonkho kwa Mfumu ya ku Roma. Amanenanso kuti ati Iyeyu ndi Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndiponso mfumu.” Pilato adafunsa Yesu kuti, “Kodi iwe, ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Yesu adati, “Mwanena nokha.” Pamenepo Pilato adauza akulu a ansembe ndi anthu onse aja kuti, “Sindikumpeza mlandu munthuyu.” Koma iwo adaumirira nati, “Ameneyu amautsa mitima ya anthu ndi zimene amaphunzitsa m'dziko lonse la Yudeya. Adayambira ku Galileya, mpaka konse kuno.” Pamene Pilato adamva zimenezi, adaŵafunsa kuti, “Kodi munthuyu ndi wa ku Galileya?” Tsono atamva kuti ngwochokeradi ku dera limene Herode amalamulira, adamtumiza kwa Herodeyo, amene nayenso anali m'Yerusalemu masiku omwewo. Herode poona Yesu, adakondwa kwambiri, chifukwa ankamva za Iye, mwakuti kwa nthaŵi yaitali ankafuna atamuwona. Ankayembekeza kuti aone Yesu akuchita chozizwitsa china. Herode adamufunsa mafunso ambiri, koma Yesu sadamuyankhe kanthu. Akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo adaimirira pomwepo nkumaneneza Yesu kwambiri. Herode pamodzi ndi asilikali ake adayamba kumseka Yesu ndi kumamnyoza. Adamuveka chovala chachifumu, namubwezera kwa Pilato. Tsiku lomwelo Herode ndi Pilato adayamba kuyanjana, chonsecho kale ankadana. Pilato adasonkhanitsa akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda ndi anthu wamba. Adaŵauza kuti, “Mwadzampereka munthuyu kwa ine kuti ndi munthu wosokeza anthu. Ndipo onani, ine ndamufunsa pamaso panu, koma sindikumpeza mlandu pa zonse zimene mukumnenezazi. Herode yemwe sadampeze mlandu, nchifukwa chake wamubweza kwa ife. Ameneyu sadachite kanthu koyenera kumuphera. Motero ndingomukwapula kenaka nkumumasula.” [ Pilatoyo ankayenera kuŵamasulira mkaidi mmodzi pa nthaŵi ya chikondwerero cha Paska.] Koma anthu onse aja adayamba kufuula pamodzi kuti, “Mchotseni ameneyu, mutimasulire Barabasi.” Barabasi anali atamponya m'ndende chifukwa cha kuyambitsa chipolowe mu mzinda, ndiponso kupha munthu. Pilato adafuna kumasula Yesu, motero adakakamba nawonso anthu aja. Koma iwo adafuulirafuulira kuti, “Mpachikeni! Mpachikeni!” Pilato adaŵafunsa kachitatu kuti, “Koma wachimwanji Iyeyu? Sindikumpeza mlandu woyenera kumuphera. Motero ndingomukwapula kenaka ndimmasula.” Koma iwo adamuumiriza mokweza mau kuti Yesu apachikidwe, kufuula kwao kunkakulirakulira. Tsono Pilato adagamula kuti zimene anthu aja ankapempha zichitike. Adaŵamasulira munthu amene ankamupempha uja, amene adaaponyedwa m'ndende chifukwa cha chipolowe ndi kupha munthu. Koma Yesu adampereka kwa iwo kuti akamchite zimene ankafuna. Asilikali adamtenga Yesu napita naye kuti akampachike. Pa njira adagwira munthu wina wa ku Kirene, dzina lake Simoni. Iye ankachokera ku midzi. Adamsenzetsa mtanda wa Yesu kuti aunyamule, azitsatira pambuyo pa Yesuyo. Anthu ambirimbiri ankamutsatira. Pakati pao panalinso akazi amene ankadzigunda pa chifuwa ndi chisoni nkumalira chifukwa cha Iye. Koma Yesu adaŵacheukira naŵauza kuti, “Inu azimai a ku Yerusalemu, musandilire Ine ai, koma mulire chifukwa cha inu nomwe ndi ana anu. Pakuti masiku akubwera pamene anthu azidzati, ‘Ngodala azimai ouma, azimai osabala, azimai amene sadayamwitseko mwana.’ Nthaŵi imeneyo adzapempha mapiri kuti, ‘Tigwereni,’ ndiponso magomo kuti, ‘Tiphimbeni.’ Pakuti ngati mtengo wauŵisi auchita zimenezi, nanga mtengo wouma ndiye adzauchita zotani?” Asilikali aja adaatenganso anthu ena aŵiri, amene anali zigaŵenga, kuti akaphedwe pamodzi ndi Yesu. Pamene adafika ku malo otchedwa Chibade cha Mutu, adapachika Yesu komweko pa mtanda. Komwekonso adapachika zigaŵenga zija, china ku dzanja lamanja, china ku dzanja lamanzere. Yesu adati, “Atate, muŵakhululukire anthuŵa, chifukwa sakudziŵa zimene akuchita.” Iwo aja adagaŵana zovala zake pakuchita maere. Anthu ena onse adaimirira pomwepo nkumaonerera. Komanso akulu a Ayuda ankamunyodola nkumanena kuti, “Adapulumutsa ena, adzipulumutse yekha ngati ndiyedi Mpulumutsi uja amene Mulungu adamsankha.” Nawonso asilikali adayamba kumseka. Adadza pafupi ndi Iye, nampatsa vinyo wosasa kuti amwe. Adati, “Ngati ndiwedi mfumu ya Ayuda, dzipulumutse wekha.” Pamwamba pa mtanda panali kalata yolembedwa m'Chigriki, m'Chilatini, ndi m'Chiyuda. Mau ake anali akuti, “Uyu ndi mfumu ya Ayuda.” Chigaŵenga chimodzi chimene chidaapachikidwa nao, chidayamba kunyoza Yesu nkumanena kuti, “Ha! Kodi iwe sindiwe Mpulumutsi Wolonjezedwa uja? Udzipulumutse wekha ndi ife tomwe.” Koma mnzake uja adamdzudzula, adati, “Kodi iwe, suwopa ndi Mulungu yemwe, chidziŵirecho kuti nawenso ukulandira chilango chomwechi? Tsonotu ife zikutiyeneradi zimenezi, tikulandira zolingana ndi zimene tidachita. Koma aŵa sadachite cholakwa chilichonse.” Ndipo adati, “Inu, mukandikumbikire mukakafika mu Ufumu wanu.” Yesu adamuyankha kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti lero lomwe lino ukhala nane ku Malo a Chisangalalo, Kumwamba.” Nthaŵi itakwana ngati 12 koloko masana, padaagwa mdima pa dziko lonse mpaka pa 3 koloko, dzuŵa litangoti bii kuda. Pamenepo chinsalu chochinga chija cha m'Nyumba ya Mulungu chidang'ambika pakatimpakati. Tsono Yesu adanena mokweza mau kuti, “Atate ndikupereka mzimu wanga m'manja mwanu.” Atanena zimenezi, adatsirizika. Mkulu wa asilikali ataona zimene zidaachitikazo, adatamanda Mulungu, adati, “Ndithudi munthuyu adaalidi wosalakwa konse.” Anthu onse amene adaasonkhana kudzaonerera zimene zinkachitikazo, ataona zonsezi, adabwerera kwao akudzigunda pa chifuwa ndi chisoni. Anthu onse amene ankadziŵana ndi Yesu, ndiponso azimai amene adaamtsatira kuchokera ku Galileya, adaima patali nkumaona zimenezi. Panali munthu wina, dzina lake Yosefe, wa ku Arimatea, mudzi wina wa Ayuda. Anali munthu wabwino ndi wolungama, ndipo anali wa m'Bungwe Lalikulu la Ayuda. Komatu sankavomereza zimene anzake a m'Bungweli ankapangana, iye ankayembekeza kudza kwa Ufumu wa Mulungu. Iyeyu adapita kwa Pilato kukapempha mtembo wa Yesu. Tsono adautsitsa naukulunga m'nsalu yoyera yabafuta, nkuuika m'manda. Mandawo anali asanaikemo munthu wina aliyense. Linali tsiku la chikonzero, tsiku la Sabata likuti liziyamba kumene. Azimai aja amene adaabwera ndi Yesu kuchokera ku Galileya, adatsatira Yosefe, naona manda ndi m'mene adaaikira mtembo wa Yesu. Kenaka adabwerera nakayamba kukonza zonunkhira ndiponso mafuta abwino. Tsono pa tsiku la Sabata adapumula malinga ndi Malamulo a Mose. M'mamaŵa pa tsiku lotsatira Sabata ya Ayuda, azimai aja adapita ku manda, atatenga zonunkhira zimene adaakakonza. Adapeza chimwala chija chili chogubuduza kale kuchoka pakhomo pa manda aja. Adaloŵa m'mandamo koma sadaupeze mtembo wa Ambuye Yesu. Akadali othedwa nzeru choncho pa zimenezo, adangoona anthu aŵiri ovala zovala zonyezimira ataimirira pafupi ndi iwo. Akazi aja adachita mantha naŵeramitsa nkhope zao pansi. Anthuwo adaŵafunsa kuti, “Mukudzafuniranji munthu wamoyo pakati pa anthu akufa? Sali muno ai, wauka. Kumbukirani zimene adaakuuzani akadali ku Galileya. Paja adaakuuzani kuti, ‘Mwana wa Munthu ayenera kuperekedwa m'manja mwa anthu ochimwa, kupachikidwa pa mtanda, ndi kuuka kwa akufa patapita masiku atatu.’ ” Apo akazi aja adaŵakumbukiradi mauwo, ndipo atabwerako kumanda kuja, adasimbira zonsezo ophunzira khumi ndi mmodzi aja, ndi anthu ena onse. Azimaiwo anali Maria wa ku Magadala, Yohana, ndi Maria, amake a Yakobe. Iwo pamodzi ndi anzao ena adasimbira atumwi aja zonsezi. Koma zimenezo atumwiwo adangoziyesa zam'kutu, mwakuti sadaŵakhulupirire azimaiwo. [ Komabe Petro adanyamuka nathamangira ku manda. Adaŵeramiramo naona nsalu zamaliro zokha, kenaka nkubwerera kunyumba akudabwa ndi zimene zidaachitikazo.] Tsiku lomwelo ophunzira aŵiri ankapita ku mudzi wotchedwa Emausi. Kuchokera ku Emausi kufika ku Yerusalemu ndi mtunda wokwanira ngati makilomita khumi ndi limodzi. Ankakambirana za zonse zimene zidaachitika. Akukambirana choncho nkumafunsana, Yesu mwiniwake adayandikira nkumatsagana nawo. Koma maso ao adaachita chidima, mwakuti sadamzindikire. Tsono Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi mukunka mukukambirana zotani panjira pano?” Apo iwo adaima, nkhope zao zili zakugwa ndi chisoni, kenaka mmodzi, dzina lake Kleopa, adamufunsa kuti, “Kodi mlendo ndinu nokha m'Yerusalemu muno, wosadziŵa zimene zachitika m'menemo masiku apitaŵa?” Yesu adaŵafunsa kuti, “Zotani?” Iwo adati, “Za Yesu wa ku Nazarete. Iye anali mneneri amene mau ake ndi zochita zake zinali zamphamvu pamaso pa Mulungu ndi pa anthu omwe. Akulu a ansembe ndi akulu athu ena adampereka kuti azengedwe mlandu ndi kuphedwa, ndipo adampachika pa mtanda. Ife tinkayembekeza kuti Iyeyo ndiye adzaombole Aisraele, koma ha! Ndi dzana pamene zidachitika zonsezi. Komanso azimai ena a m'gulu lathu anatidabwitsa. Iwowo anapita ku manda m'mamaŵa, ndiye amati sadaupeze mtembo wake. Tsono atabwerako amadzasimba kuti anaona angelo amene anaŵauza kuti Yesu ali moyo. Ena mwa ife anapita kumandako, ndipo anakapezadi monga momwe azimai aja amasimbira, koma Iyeyo sadamuwone ai.” Apo Yesu adati, “Ha! Koma ndiye ndinu anthu opusa, osafuna kukhulupirira msanga zonse zija zimene aneneri adanena. Kodi inu simukudziŵa kuti Mpulumutsi wolonjezedwa uja adaayenera kumva zoŵaŵa zonsezi kuti aloŵe mu ulemerero wake?” Kenaka Yesu adayamba kuŵatanthauzira zimene zidalembedwa za Iye m'Malembo onse, kuyambira pa mabuku a Mose mpaka mabuku a aneneri onse. Atayandikira kumudzi kumene ankapita, Yesu adachita ngati akupitirira. Koma iwo adamuumiriza kuti, “Mukhale nafe konkuno, poti kwayamba kuda; onani dzuŵa likuloŵa.” Apo Iye adakaloŵa m'nyumba nakakhala nawo. Pamene adakhala nawo podyera, Yesu adatenga buledi, ndipo atathokoza Mulungu, adamnyema naŵagaŵira. Nthaŵi yomweyo maso ao adatsekuka, namuzindikira, Iye nkuzimirira. Tsono iwo adayamba kukambirana kuti, “Zoonadi ndithu, mitima yathu inachita kuti phwii, muja amalankhula nafe panjira paja, nkumatitanthauzira Malembo.” Nthaŵi yomweyo adanyamuka kubwerera ku Yerusalemu. Adakapeza ophunzira khumi ndi mmodzi aja atasonkhana pamodzi ndi anzao ena, akunena kuti, “Ambuye adaukadi, ndipo Simoni waŵaona.” Tsono nawonso aŵiri aja adafotokoza zimene zidaachitika panjira paja, ndiponso m'mene iwo adaamzindikirira pamene Iye ankanyema buledi. Iwo akulankhula choncho, Yesu mwiniwake adadzaimirira pakati pao nati, “Mtendere ukhale nanu.” Koma iwo adadzidzimuka, nkuchita mantha poyesa kuti akuwona mzukwa. Tsono Yesu adati, “Mukuvutikiranji, mukudzipheranji ndi mafunso m'mitima mwanu? Onani manja anga ndi mapazi anga, kuti ndine ndithu. Khudzeni muwone, paja mzukwa ulibe mnofu ndi mafupa monga mukuwona kuti Ine ndili nazo.” Atanena zimenezi adaŵaonetsa manja ake ndi mapazi ake. Iwo sankakhulupirirabe chifukwa cha chimwemwe, ndipo adaathedwa nzeru. Tsono Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi pano muli nako kanthu kakudya?” Adampatsa chidutsu cha nsomba yootcha. Iye atalandira nsombayo, adaidya iwo akuwona. Kenaka adaŵauza kuti, “Nzimenezitu zimene ndinkakuuzani pamene ndinali nanu. Paja ndinkanena kuti zonse ziyenera kuchitikadi zimene zidalembedwa za Ine m'Malamulo a Mose, m'mabuku a aneneri, ndi m'buku la Masalimo.” Tsono adaŵathandiza kuti amvetse bwino Malembo. Adaŵauza kuti, “Zimene zidalembedwa ndi izi: zakuti Mpulumutsi wolonjezedwa uja adayenera kumva zoŵaŵa, nkuuka kwa akufa patapita masiku atatu, kuti m'dzina lake mau alalikidwe kwa anthu a mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu, mau akuti atembenuke mtima, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao. Inuyo ndinu mboni zake za zimenezi. Ine ndidzakutumizirani mphatso imene Atate anga adalonjeza. Koma inu bakhalani mumzinda muno mpaka mutalandira mphamvu zochokera Kumwamba.” Atatero Yesu adaŵatsogolera kuchokera mumzindamo mpaka ku mudzi wa Betaniya. Kumeneko adakweza manja ake naŵadalitsa. Akuŵadalitsa choncho, adalekana nawo, natengedwa kupita Kumwamba. Iwo adampembedza, pambuyo pake nkubwerera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu. Tsono ankasonkhana m'Nyumba ya Mulungu nthaŵi ndi nthaŵi akutamanda Mulungu. Pachiyambi pa zonse Iye amene amatchedwa dzina loti Mau, anali alipo kale. Anali kwa Mulungu, ndipo anali Mulungu. Anali kwa Mulungu chikhalire. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, ndipo palibe chilichonse chimene chidalengedwa popanda Iye. Mwa Iyeyo munali moyo, ndipo moyowo unali kuŵala kounikira anthu. Kuŵalako kukuunikabe mu mdima, ndipo mdima sudathe kugonjetsa kuŵalako. Mulungu adaatuma munthu wina, dzina lake Yohane. Iyeyu adaabwera ngati mboni, kudzachitira umboni kuŵala kuja, kuti anthu onse akhulupirire chifukwa cha umboni wakewo. Sikuti iyeyo ndiye anali kuŵalako ai, koma adangobwera kudzachitira umboni kuŵalako. Kuŵala kwenikweni, kounikira anthu onse, kunkadza pansi pano. Wotchedwa Mauyo anali m'dziko lapansi, ndipo Mulungu adalenga dziko lapansilo kudzera mwa Iye, komabe anthu apansipano sadamzindikire. Adaabwera kwao ndithu, koma anthu ake omwe sadamlandire. Komabe ena adaamlandira nakhulupirira dzina lake, ndipo ameneŵa Iye adaŵapatsa mphamvu zoti akhale ana a Mulungu. Kukhala ana a Mulungu kumeneku sikudachokere m'kubadwa kwao, kapena ku chifuniro cha thupi, kapena ku chifuniro cha munthu ai, koma kudachokera kwa Mulungu. Wotchedwa Mau uja adasanduka munthu, nadzakhala pakati pathu. Anali wokoma mtima ndi wokhulupirika kwabasi. Ndipotu tidaona ulemerero wake, ndiye kuti ulemerero womwe Iye amalandira kwa Atate pokhala Mwana wao mmodzi yekha uja. Yohaneyo adaamchitira umboni. Ankauza anthu mwamphamvu kuti, “Uyu ndiye uja ndinkanenayu kuti amene akubwera pambuyo panga ngwoposa ine; pakuti ine ndisanabadwe, Iye alipo.” Kuchokera m'kukoma mtima kwake kwathunthu ife tonse tidalandira madalitso, madalitso ake otsatanatsatana. Paja Mulungu adatipatsa Malamulo ake kudzera mwa Mose, koma kudzera mwa Yesu Khristu adatizindikiritsa kukoma mtima ndi kukhulupirika kwake. Chikhalire palibe munthu amene adaona Mulungu, koma Mwana mmodzi yekha uja, amene ali wapamtima wa Atate, ndiye adaulula za Mulunguyo. Nthaŵi ina akuluakulu a Ayuda a ku Yerusalemu adaatuma ansembe ndi Alevi ena kukafunsa Yohane kuti, “Kodi iwe ndiwe yani?” Iye adayankha mosabisa konse, adanenetsa ndithu kuti, “Inetu sindine Mpulumutsi wolonjezedwa uja ai.” Adamufunsanso kuti, “Nanga ndiwe yani? Ndiwe Eliya kodi?” Iye adati, “Iyai, sindine Eliya.” Iwo adati, “Kodi ndiwe Mneneri tikumuyembekeza uja?” Koma Yohane adayankha kuti, “Ainso.” Tsono adamuuza kuti, “Tanena zenizenitu, kuti tikaŵafotokozere bwino amene atituma. Mwiniwakewe umati ndiwe yani?” Yohane adaŵayankha kuti, “Monga adaanenera mneneri Yesaya: “Ine ndine liwu la munthu wofuula m'chipululu; akunena kuti, ‘Ongolani mseu wodzadzeramo Ambuye.’ ” Anthu aja adaaŵatuma ndi Afarisi. Tsono adafunsa Yohane kuti, “Ngati sindiwe Mpulumutsi wolonjezedwa uja, kapena Eliya, kapenanso Mneneri tikumuyembekeza uja, nanga bwanji umabatiza?” Yohane adaŵayankha kuti, “Ine ndimabatiza ndi madzi, koma pakati panupa pali wina amene inu simukumdziŵa. Iyeyu ngwobwera pambuyo panga, komabe sindili woyenera ngakhale kumasula zingwe za nsapato zake.” Zimenezi zidachitikira ku Betaniya, kutsidya kwa mtsinje wa Yordani, kumene Yohane ankabatiza. M'maŵa mwake Yohane adaona Yesu akubwera kwa iye, ndipo adati, “Suuyu Mwanawankhosa wa Mulungu uja, wochotsa machimo a anthu a pa dziko lonse lapansi. Iyeyu ndi amene ndinkanena uja kuti, ‘Pambuyo panga pakubwera munthu wopambana ine, pakuti ine ndisanabadwe, Iye alipo.’ Inenso sindinkamudziŵa, koma ndidabwera kudzabatiza ndi madzi kuti Aisraele amdziŵe.” Yohane adachitanso umboni, adati, “Ndidaona Mzimu Woyera akutsika kumwamba ngati nkhunda, nakhazikika pa Iye. Ine sindinkamudziŵa, koma Mulungu amene adandituma kudzabatiza ndi madzi, ndiye adaandiwuza kuti, ‘Amene udzaone Mzimu Woyera akutsika ndi kukhazikika pa Iye, ndi Iyeyo wobatiza mwa Mzimu Woyera.’ Ineyo ndidaziwonadi, ndipo ndikuchita umboni kuti ameneyu ndi Mwanadi wa Mulungu.” M'maŵa mwakenso Yohane anali pamalo pomwepo pamodzi ndi ophunzira ake ena aŵiri. Pamene adaona Yesu akuyenda, iye adati, “Suuyu Mwanawankhosa wa Mulungu.” Ophunzira aŵiri aja atamva mauwo, adatsatira Yesu. Yesu adacheuka naona kuti akumtsatira, tsono adaŵafunsa kuti, “Kodi ulendowu?” Iwo adati, “Timati tidziŵe, kodi mumakhala kuti, Rabi?” (Tanthauzo la Rabi ndiye kuti, Mphunzitsi.) Yesu adati, “Tiyeni mukakuwone.” Iwo adapita naye. Pamenepo nthaŵi inali ngati 4 koloko madzulo. Adakaonako kumene Iye ankakhala, ndipo adakhala naye tsiku limenelo. Mmodzi mwa aŵiri aja amene adaamva mau a Yohane natsatira Yesu, anali Andrea, mbale wake wa Simoni Petro. Iye adayamba kukapeza mbale wakeyo Simoni, namuuza kuti, “Tampeza Mesiya.” (Ndiye kuti, Mpulumutsi wolonjezedwa uja.) Motero adamtenga kupita naye kwa Yesu. Pamene Yesu adamuwona adati, “Ndiwe Simoni, mwana wa Yohane. Dzina lako lidzakhala Kefa.” (Tanthauzo la Kefa ndi Petro, ndiye kuti Thanthwe.) M'maŵa mwake Yesu adaganiza zopita ku Galileya. Adapeza Filipo, namuuza kuti, “Unditsate.” Filipo anali wa ku mudzi wa Betsaida, kwaonso kwa Andrea ndi Petro. Filipo adakapeza Natanaele namuuza kuti, “Tampeza Ujayu amene Mose adalemba za Iye m'buku la Malamulo, uja anenerinso adalemba za Iye. Ndi Yesu Mwana wa Yosefe, wa ku Nazarete.” Koma Natanaele adamufunsa kuti, “Kodi ku Nazarete nkuchokera kanthu kabwino?” Filipo adati, “Tiye ukadziwonere wekha.” Pamene Yesu adaona Natanaele akubwera potero, adati, “Mwamuwonatu Mwisraele weniweni wopanda chinyengo.” Natanaele adamufunsa kuti, “Mwandidziŵa bwanji?” Yesu adati, “Muja unakhala patsinde pa mkuyu paja, Filipo asanakuitane, Ine ndinakuwona.” Natanaele adati, “Aphunzitsi, ndinudi Mwana wa Mulungu, ndinu Mfumu ya Israele.” Yesu adamuyankha kuti, “Kodi wakhulupirira chifukwa ndakuuza kuti ndinakuwona patsinde pa mkuyu paja? Udzaona zoposa pamenepa.” Adatinso, “Ndithu ndikunenetsa kuti mudzaona Kumwamba kutatsekuka, angelo a Mulungu akukwera ndi kutsika pa Mwana wa Munthu.” Patapita masiku aŵiri, kunali ukwati ku mudzi wa Kana m'dera la Galileya. Amai ake a Yesu anali komweko. Yesu nayenso pamodzi ndi ophunzira ake adaaitanidwa kuukwatiko. Pamene vinyo adatha, amai ake a Yesu adamuuza kuti, “Waŵathera vinyo.” Yesu adayankha kuti, “Mai, kodi mukuti nditani? Nthaŵi yangatu siinafike.” Apo amai ake adauza anyamata amene ankatumikira kuti, “Chilichonse chimene akuuzeni, muchite.” Pamenepo panali mbiya zamwala zisanu ndi imodzi, zimene adaaziikapo chifukwa cha mwambo wa kudziyeretsa wa Ayuda. M'mbiya iliyonse munkaloŵa madzi okwanira malita zana limodzi kapena kupitirirapo. Tsono Yesu adauza anyamata aja kuti, “Dzazani mbiyazi ndi madzi.” Ndipo adazidzaza mpaka m'milomo. Pambuyo pake adaŵauza kuti, “Tsopano tungani, kaperekeni kwa mkulu wa phwando,” Iwowo adakaperekadi. Mkulu wa phwandoyo adalaŵa madzi osanduka vinyowo osadziŵa kumene achokera. (Koma anyamata aja amene adaatunga madziwo ankadziŵa.) Tsono mkulu wa phwandoyo adaitana mkwati, namuuza kuti, “Anzanu amapereka vinyo wabwino kwambiri poyamba, kenaka anthu atakhuta, amaŵapatsa vinyo wokoma pang'ono. Koma inu mwasunga vinyo wabwino kwambiri kufikira tsopano.” Yesu adaonetsa chizindikiro chake choyambachi m'mudzi wa Kana m'dera la Galileya. Pamenepo adaonetsa ulemerero wake, ndipo ophunzira ake adamkhulupirira. Pambuyo pake Yesu adapita ku Kapernao, pamodzi ndi amai ake ndi abale ake ndi ophunzira ake, ndipo adakhala kumeneko masiku oŵerengeka. Itayandikira nthaŵi ya Paska, chikondwerero cha Ayuda, Yesu adanyamuka kupita ku Yerusalemu. Kumeneko adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu napezamo anthu akugulitsa ng'ombe, nkhosa ndi nkhunda. Munalinso anthu osinthitsa ndalama. Apo Yesu adapanga mkwapulo wazingwe nayamba kuŵatulutsira onse kunja, pamodzi ndi nkhosa ndi ng'ombe zao zomwe. Adagubudula matebulo a osinthitsa ndalama aja, naŵamwazira ndalama zao. Ndipo adalamula ogulitsa nkhunda aja kuti, “Izi zitulutseni muno. Nyumba ya Atate anga musaisandutse nyumba yochitiramo malonda.” Ophunzira ake adakumbukira Malembo aja akuti, “Changu chomwe ndimachitira nyumba yanu chidzandiphetsa.” Pamenepo akuluakulu a Ayuda adamufunsa kuti, “Kodi mungatiwonetse chizindikiro chotani chakuti muli ndi ulamuliro wochitira zimenezi?” Yesu adaŵayankha kuti, “Gwetsani nyumba ya Mulungu ino, Ine ndidzaimanganso masiku atatu.” Apo iwo adati, “Nyumba ya Mulunguyi idatenga zaka 46 kuti aimange, tsono Inu nkuimanga masiku atatu chabe?” Koma Yesu ankanena za thupi lake mophiphiritsa, pamene adaatchula Nyumba ya Mulungu. Iye atauka kwa akufa, ophunzira ake adadzakumbukira kuti adaanena zimenezi, nakhulupirira Malembo ndiponso mau amene Yesu adaanenawo. Pamene Yesu anali m'Yerusalemu pa chikondwerero cha Paska, anthu ambiri adayamba kuika chikhulupiriro chao pa Iye, poona zozizwitsa zimene ankachita. Koma Yesu sadaikepo chikhulupiriro pa iwowo, popeza kuti Iye ankaŵadziŵa anthu onse. Sankalira kuti wina achite chomuuza za munthu aliyense. Pakuti mwiniwakeyo ankadziŵa za m'mitima mwa anthu. Munthu wina wa m'gulu la Afarisi, dzina lake Nikodemo, mkulu wa Ayuda, adadza kwa Yesu usiku. Adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, tikudziŵa kuti ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu, pakuti palibe munthu wotha kuchita zizindikiro zozizwitsa zimene Inu mukuzichita, ngati Mulungu sali naye.” Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti ngati munthu sabadwanso kwatsopano, sangauwone Ufumu wa Mulungu.” Nikodemo adamufunsa kuti, “Kodi munthu angathe kubadwanso bwanji atakalamba kale? Kodi nkukaloŵa m'mimba mwa amai ake kuti abadwe kachiŵiri?” Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti ngati munthu sabadwa m'madzi ndi mwa Mzimu Woyera, sangathe kuloŵa mu Ufumu wa Mulungu. Chobadwa mwa munthu ndi thupi chabe, koma chobadwa mwa Mzimu Woyera ndi mzimu. Usadabwe m'mene ndakuuza kuti muyenera kubadwanso. Mphepo imaombera komwe ikufuna, ndipo umamva kuwomba kwake, koma sudziŵa komwe yachokera kapena komwe ikupita. Nchimodzimodzi munthu aliyense amene abadwa mwa Mzimu Woyera.” Nikodemo adafunsa kuti, “Zimenezi zingachitike bwanji?” Yesu adati, “Kodi iwe sindiwe mphunzitsi wodziŵika pakati pa Aisraele, nanga sukumvetsa bwanji zimenezi? Ndithu ndikunenetsa kuti timalankhula zimene tikuzidziŵa, ndipo timachitira umboni zimene tidaziwona, koma inu simukukhulupirira mau athuŵa. Ngati simukhulupirira pamene ndikukuuzani zapansipano, nanga mudzakhulupirira bwanji ndikadzakuuzani za Kumwamba? Palibe munthu amene adakwera kupita Kumwamba, koma Mwana wa Munthu ndiye adatsika kuchokera Kumwamba. “Monga momwe Mose adaapachikira njoka pa mtengo m'chipululu muja, momwemonso Mwana wa Munthu ayenera kudzapachikidwa, kuti aliyense wokhulupirira akhale ndi moyo wosatha mwa Iye. Mulungutu adaŵakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha. Mulungu adatuma Mwana wakeyo pansi pano, osati kuti adzazenge anthu mlandu, koma kuti adzaŵapulumutse. “Munthu wokhulupirira Mwanayo, sazengedwa mlandu. Koma wosakhulupirira, wazengedwa kale, chifukwa sadakhulupirire Mwana mmodzi yekha uja wa Mulungu. Mlandu wake ndi uwu wakuti ngakhale kuŵala kudadza pansi pano, anthu adakonda mdima, osati kuŵalako, chifukwa zochita zao zinali zoipa. Aliyense wochita zoipa, amadana ndi kuŵala. Saonekera poyera, kuwopa kuti zochita zakezo zingaonekere. Koma wochita zokhulupirika amaonekera poyera, ndipo zochita zake zimadziŵika kuti wazichita momvera Mulungu.” Pambuyo pake Yesu ndi ophunzira ake adapita ku dera la Yudeya. Adakhala nawo kumeneko kanthaŵi, ndipo ankabatiza. Yohane nayenso ankabatiza ku Ainoni pafupi ndi Salimu, chifukwa kumeneko kunali madzi ambiri. Anthu ankafikako, iye nkumaŵabatiza. Pamenepo nkuti Yohane asanaponyedwe m'ndende. Ophunzira ena a Yohane adayamba kukangana ndi Myuda wina pa za mwambo wa kuyeretsa. Choncho ophunzirawo adadza kwa Yohane namuuza kuti, “Aphunzitsi onanitu, munthu uja amene anali ndi inu patsidya pa Yordani, yemwe uja munkamuchitira umboniyu, nayenso akubatiza, ndipo anthu onse akuthamangira kwa Iye.” Yohane adati, “Munthu sangalandire kanthu kalikonse ngati Mulungu sampatsa. Inu nomwe ndinu mboni zanga kuti ndidati, ‘Sindine Mpulumutsi wolonjezedwa uja, koma ndine wotumidwa patsogolo pake.’ Mkwati wamkazi mwini wake ndi mkwati wamwamuna. Koma bwenzi la mkwati wamwamuna limaimirira pafupi, nkumamvetsera. Limakondwa kwakukulu likamva mau a mkwati wamwamunayo. Momwemonso ine ndakondwa kwakukulu. Iye uja ayenera kumakula, ine nkumachepa.” “Wochokera Kumwamba ali pamwamba pa onse. Wochokera pansi pano ndi wapansipano, ndipo amalankhula zapansipano. Wochokera Kumwamba ali pamwamba pa onse. Iyeyu akuchitira umboni zimene adaziwona ndi kuzimva komabe palibe amene amakhulupirira mau akewo. Koma munthu akakhulupirira mau akeŵo, pamenepo amatsimikiza kuti Mulungu sanama. Amene Mulungu adamtumayo, amalankhula mau a Mulungu, pakuti Mulungu amapereka Mzimu Woyera mosaumira. Mulungu Atate amakonda Mwana wake, ndipo adaika zonse m'manja mwake. Munthu wokhulupirira Mwanayo, ali ndi moyo wosatha. Koma wokana kukhulupirira Mwanayo, sadzaona moyo, chifukwa chilango cha Mulungu chili pa iye.” Afarisi adamva kuti Yesu akukopa ndi kubatiza ophunzira ambiri koposa Yohane. (Komabe amene ankabatiza si Yesuyo, koma ophunzira ake). Pamene Yesu adadziŵa kuti Afarisi azimva zimenezi, adachokako ku Yudeya napitanso ku Galileya. Pa ulendowo ankayenera kudzera m'dziko la Samariya. Tsono adafika ku mudzi wina wa ku Samariya, dzina lake Sikari, pafupi ndi kadziko kamene Yakobe adaapatsa Yosefe, mwana wake. Kumeneko kunali chitsime cha Yakobe. Yesu adakhala pansi pambali pa chitsimecho, chifukwa anali atatopa ndi ulendo. Nthaŵi inali ngati 12 koloko masana. Tsono padafika mai wina wachisamariya kudzatunga madzi. Yesu nkunena mopempha kuti, “Zikomo mundipatseko madzi akumwa.” Nthaŵiyo nkuti ophunzira ake aja atakagula chakudya mu mzinda. Mai wachisamariya uja adayankha nati, “Inu amene muli Myuda, bwanji mukupempha madzi kwa ine, mai wachisamariya?” (Pakutitu Ayuda sayenderana ndi Asamariya.) Yesu adati, “Mukadadziŵa mphatso ya Mulungu, mukadadziŵanso amene akupempha madzi akumwayu, bwenzi mutampempha ndi inuyo mai, Iye nakupatsani madzi opatsa moyo.” Maiyo adati, “Bambo, mulibe nchotungira chomwe, ndipo chitsimechi nchozama. Nanga madzi opatsa moyowo muŵatenga kuti? Yakobe, kholo lathu ndiye adatipatsa chitsimechi, chimene mwiniwakeyo ankamwapo pamodzi ndi ana ake, ndiponso zoŵeta zake. Kodi Inu mungapambane iyeyo?” Yesu adati, “Munthu aliyense womwako madzi aŵa, adzamvanso ludzu. Koma aliyense wodzamwa madzi amene Ine ndidzampatse, sadzamvanso ludzu konse mpaka muyaya. Madzi amene ndidzampatsewo azidzatumphukira mwa iye ngati kasupe wa madzi opatsa moyo, nkumupatsa moyo wosatha.” Maiyo adati, “Bambo, patsaniko ineyo madzi amenewo kuti ndisamamvenso ludzu kapena kumadzatunganso madzi kuno.” Yesu adati, “Pitani mukaitane amuna anu, nkukabweranso kuno.” Maiyo adati, “Ndilibe mwamuna.” Yesu adati, “Mwanenetsa kuti mulibe mwamuna. Paja mwakwatiwapo kale ndi amuna asanu, ndipo mwamuna amene muli naye tsopano si wanunso. Mwanenazi nzoona.” Maiyo adati, “Bambo, ndadziŵa tsopano kuti ndinu mneneri. Makolo athu ankapembedza Mulungu pa phiri ili, koma inu Ayuda mumati ndi ku Yerusalemu kumene anthu ayenera kumakapembedzerako.” Yesu adamuuza kuti, “Mai, ndithu ikudza nthaŵi pamene mudzapembedza Atate, osati pa phiri ili kapenanso ku Yerusalemu ai. Asamariyanu mumapembedza chimene simuchidziŵa. Ayudafe timapembedza chimene timachidziŵa, pakuti chipulumutso nchochokera mwa Ayuda. Koma ikudza nthaŵi, ndipo yafika kale, pamene anthu opembedza kwenikweni adzapembedza Atate mwauzimu ndi moona. Atate amafuna anthu otere kuti ndiwo azimpembedza. Mulungu ndi mzimu, ndipo ompembedza Iye ayenera kumpembedza mwauzimu ndi moona.” Maiyo adati, “Ndikudziŵa kuti akudza Mpulumutsi wolonjezedwa uja. Iyeyo akadzafika, adzatifotokozera zonse.” Yesu adamuuza kuti, “Ndine amene, Ineyo amene ndikulankhula nanu, mai.” Nthaŵi yomweyo ophunzira ake a Yesu adafika, ndipo ankadabwa kuti Iye akucheza ndi mkazi. Komabe panalibe amene adamufunsa kuti, “Zakhala bwanji?” Kapena kuti, “Bwanji mukulankhula naye?” Maiyo adasiya mtsuko wake napita ku mudzi nkukauza anthu kuti, “Tiyeni, mukaone munthu amene wandiwuza zonse zimene ine ndidachita. Kodi ameneyu sangakhale Mpulumutsi wolonjezedwa uja kapena?” Apo anthuwo adatuluka m'mudzimo kubwera kwa Yesu, Nthaŵi imeneyo ophunzira ake a Yesu ankamupempha kuti, “Aphunzitsi, idyani.” Koma Iye adati, “Ine ndili nacho chakudya chimene inu simukuchidziŵa.” Pamenepo ophunzirawo adayamba kufunsana kuti, “Kodi kapena wina wadzaŵapatsa kale chakudya?” Koma Yesu adati, “Chakudya changa nkuchita zimene afuna Atate amene adandituma, kuti nditsirize ntchito imene Iwo adandipatsa. Paja anthu amati, ‘Ikapita miyezi inai, ndiye kuti yafika nyengo yokolola.’ Koma ndithu, taonani m'mindamu, kodi simukuwona kuti mbeu zacha kale kudikira kholola? Okolola ayamba kale kulandira malipiro, ndipo akututira mbeu ku moyo wosatha, kuti obzala ndi okolola akondwere pamodzi. Paja amanenadi zoona aja amati, ‘Wobzala ndi wina, wokolola ndi winanso.’ Ine ndidakutumani kukakolola mbeu zimene simudagwirirepo ntchito. Anthu ena ndiwo adagwira ntchito, inu mwangolandirapo phindu la ntchito yaoyo.” Asamariya ambiri a m'mudzi muja adakhulupirira Yesu chifukwa cha umboni wa mai uja, wakuti, “Iye wandiwuza zonse zimene ndidachita.” Tsono pamene Asamariyawo adafika kwa Yesu, adampempha kuti akhale nao kwaoko. Ndipo adakhaladi komweko masiku aŵiri. Pamenepo anthu enanso ambiri adakhulupirira chifukwa cha mau a Yesu. Mwakuti adauza mai uja kuti, “Takhulupirira tsopano, osati chifukwa cha mau ako, koma chifukwa tadzimvera tokha. Tadziŵa kuti ameneyu ndi Mpulumutsidi wa anthu a pa dziko lonse lapansi.” Atapita masiku aŵiriwo, Yesu adachoka napita ku Galileya. Mwiniwakeyo anali atanena kuti, “Mneneri, anthu akwao samchitira ulemu.” Komabe pamene adafika ku Galileya, Agalileya adamlandira popeza kuti eniakewo nawonso adaapita ku Yerusalemu ku chikondwerero cha Paska, ndipo adaaona zonse zimene Yesu adaachita pachikondwereropo. Yesu adapitanso ku mudzi wa Kana ku Galileya, kumene Iye adaasandutsa madzi vinyo kuja. Panali Nduna ina ya mfumu imene mwana wake ankadwala ku Kapernao. Pamene adamva kuti Yesu wafika ku Galileya kuchokera ku Yudeya, adadza kwa Iye nampempha kuti apite naye ku Kapernao, kuti akachiritse mwana wake amene anali pafupi kufa. Yesu adamuuza kuti, “Mukapanda kuwona zizindikiro ndi zozizwitsa, simukhulupirira ai.” Ndunayo idati, “Ndapota nanu Ambuye, tiyeni mwana wanga asanafe.” Yesu adamuuza kuti, “Pitani! Mwana wanu wachira.” Munthuyo adakhulupiriradi mau a Yesuwo, ndipo adapita kwao. Pa njira adakumana ndi antchito ake, ndipo iwo adamuuza kuti, “Mwana wanu wachira.” Adaŵafunsa za nthaŵi imene adachira mwanayo, iwo nkunena kuti, “Malungo ake adamleka dzulo nthaŵi ya 1 koloko masana.” Bamboyo adazindikira kuti inali nthaŵi yomwe Yesu adaamuuza kuti, “Mwana wanu wachira.” Tsono iye adakhulupirira pamodzi ndi onse a m'banja mwake. Ichi chinali chizindikiro chachiŵiri chimene Yesu adaonetsa atafika ku Galileya kuchokera ku Yudeya. Pambuyo pake kunali chikondwerero chachipembedzo cha Ayuda, ndipo Yesu adapitako ku Yerusalemuko. Kumeneko kuli dziŵe, dzina lake pa Chiyuda ndi Betesida. Dziŵeli lili pafupi ndi Chipata cha Nkhosa, ndipo nlozingidwa ndi makonde asanu. M'makondemo munkagona anthu ambiri odwala, akhungu, opunduka miyendo ndi opuwala ziwalo. [Iwoŵa ankadikira kuti madzi agwedezeke. Pakuti nthaŵi zina mngelo wa Ambuye ankatsikira m'dziŵemo nkuvundula madziwo. Woyamba kuloŵamo madzi atavundulidwa, ankachira ngakhale akhale ndi nthenda yanji.] Pakati pa anthu odwalawo panali wina amene adaadwala zaka 38. Yesu adamuwona ali gone, nadziŵa kuti adaadwala nthaŵi yaitali. Tsono adamufunsa kuti, “Kodi ukufuna kuchira?” Wodwalayo adati, “Ambuye, ndilibe munthu wondiloŵetsa m'dziŵemu madzi akavundulidwa. Ndikati ndiloŵemo, wina waloŵa kale.” Yesu adamlamula kuti, “Dzuka, tenga mphasa yako, yamba kuyenda.” Pompo munthuyo adachiradi, nanyamula mphasa yake nkuyamba kuyenda. Tsikulo linali la Sabata. Choncho Ayuda adauza munthu amene adachirayo kuti, “Lero mpa Sabata. Malamulo athu sakulola kunyamula mphasa yako.” Koma iye adati, “Amene wandichiritsa ndiye wandiwuza kuti, ‘Nyamula mphasa yako, yenda.’ ” Iwo adamufunsa kuti, “Munthuyo ndani amene wakuuza kuti unyamule mphasa yako, uyende?” Koma wochirayo sadamdziŵe, popeza kuti Yesu anali ataloŵerera m'kati mwa anthu ambiri amene anali pamenepo. Pambuyo pake Yesu adapeza wochira uja m'Nyumba ya Mulungu, namuuza kuti, “Ona, wachira tsopano. Usakachimwenso, kuti chingakugwere choopsa china kuposa pamenepa.” Munthuyo adapita nakauza Ayuda kuti Yesu ndiye amene wamchiritsa. Popeza kuti linali tsiku la Sabata pamene Yesu adaachita zimenezi, Ayuda adayamba kumuvutitsa. Koma Yesu adaŵauza kuti, “Atate anga akugwira ntchito mpaka tsopano, nanenso ndikugwira ntchito.” Pamenepo ndiye Ayuda adankirankira kufuna kumupha. Ankati Yesu akuphwanya lamulo lokhudza Sabata, ndiponso ponena kuti Mulungu ndi Atate ake, ankadzilinganiza ndi Mulungu. Tsono Yesu adati, “Kunena zoona Ine Mwanane sindingathe kuchita kanthu pandekha. Ndimangochita zimene ndikuwona Atate anga akuchita. Zimene Atate amachita, Mwana amachitanso zomwezo. Pakuti Atate amakonda Mwana, namuwonetsa zonse zimene Iwo akuchita. Atate adzamuwonetsanso ntchito zoposa zimenezi, kuti inu muzizwe. Monga Atate amaukitsa akufa, naŵapatsa moyo, moteronso Mwana amapatsa moyo kwa amene Iye afuna. Atate saweruza munthu aliyense, koma adaika Mwana wake kuti akhale woweruza pa zonse. Atate amafuna kuti anthu onse azilemekeza Mwana, monga momwe amalemekezera Atate. Munthu amene salemekeza Mwana, salemekezanso Atate amene adamtuma. “Ndithu ndikunenetsa kuti munthu womva mau anga, nakhulupirira Iye amene adandituma, ameneyo ali ndi moyo wosatha. Iyeyo sazengedwa mlandu, koma watuluka kale mu imfa, ndipo waloŵa m'moyo. Ndikunenetsanso kuti ikudza nthaŵi, ndipo yafika kale, pamene anthu amene ali ngati akufa adzamva mau a Mwana wa Mulungu, ndipo amene adzaŵakhulupirira adzakhala ndi moyo. Monga Atate ali gwelo la moyo, momwemonso adaika Mwana wake kuti nayenso akhale gwelo la moyo. Ndipo adapatsa Mwanayo mphamvu ya kuweruza anthu, chifukwa ndi Mwana wa Munthu. Musadabwe nazo zimenezi, pakuti ikudza nthaŵi pamene anthu onse amene ali m'manda adzamva mau ake nadzatuluka. Anthu amene adachita zabwino, adzauka kuti akhale ndi moyo, koma amene adachita zoipa, adzauka kuti azengedwe mlandu.” “Ine sindingathe kuchita kanthu pandekha. Ndimaweruza monga momwe Atate amandiwuzira. Ndipo ndimaweruza molungama, popeza kuti sinditsata zimene ndifuna Ineyo, koma zimene afuna Atate amene adandituma. “Ngati ndidzichitira ndekha umboni, umboni wangawo ngwosakwanira. Pali wina wondichitira umboni, ndipo ndikudziŵa kuti umboni umene iye amandichitirawo ngwoona. Inu nomwe mudaatuma amithenga anu kwa Yohane Mbatizi, ndipo iye adachitira umboni choona. Sikuti Ine ndikudalira umboni wa munthu, koma ndikunena izi kuti inu mupulumuke. Yohane anali ngati nyale yoyaka ndi yoŵala, ndipo inu mudafuna kukondwerera kuŵala kwakeko pa kanthaŵi. Koma Ine ndili ndi umboni woposa wa Yohane. Atate adandipatsa ntchito zimene ndiyenera kuzichita, ndipo ntchito ndikuchitazi zikutsimikiza kuti Atate ndiwo adandituma. Ndipo Atate omwewo amene adandituma, adandichitira umboni. Koma inu simudamve konse liwu lao, maonekedwe aonso simudaŵaone. Mau ao sakhala mwa inu, chifukwa simumkhulupirira amene Atatewo adamtuma. Mumaphunzira Malembo mozama, chifukwa mumaganiza kuti mupezamo moyo wosatha. Ndipotu ndi Malembo omwewo amene akundichitira umboni! Komabe inu simufuna kudza kwa Ine kuti mukhale ndi moyo. “Sindikufunafuna ulemu wa anthu ai. Koma ndikukudziŵani, mulibe chikondi cha Mulungu mumtima mwanu. Ine ndidadza m'dzina la Atate anga, ndipo inu simukundilandira. Koma wina atabwera m'dzina la iye yekha, iyeyo ndiye mungamlandire. Mukamapatsana ulemu nokhanokha mumasangalala, koma simufuna konse kulandira ulemu wochokera kwa amene Iye yekha ndiye Mulungu. Nanga mungakhulupirire bwanji? Musayese kuti ndine amene ndidzakunenezeni kwa Atate, ai. Wodzakunenezani alipo. Ndi Mose yemwe uja amene inu mumamdalira. Mukadakhulupirira Mose moona, bwenzi mutakhulupiriranso Ine, pakuti iye adaalemba za Ine. Koma ngati simukhulupirira zimene iyeyo adalemba, nanga mungakhulupirire bwanji mau anga?” Pambuyo pake Yesu adaoloka nyanja ya Galileya (dzina lake lina ndi nyanja ya Tiberiasi.) Khamu lalikulu la anthu lidamtsatira, chifukwa lidaaona zizindikiro zozizwitsa zimene adaachita pakuchiritsa anthu odwala. Yesu adakwera m'phiri nakhala pansi ndi ophunzira ake. Chikondwerero chija chachipembedzo chotchedwa Paska chidaayandikira. Pamene Yesu adayang'ana, adaona khamu lalikulu la anthu lija likudza kwa Iye. Tsono Iye adafunsa Filipo kuti, “Kodi tingakagule kuti chakudya chodyetsa anthu onseŵa?” (Adaafunsa zimenezi dala kuti amuyese Filipoyo, koma mwiniwakeyo adaadziŵiratu choti achite.) Filipo adayankha kuti, “Ngakhale ndalama mazana aŵiri sizingakwanire konse kugula chakudya choti aliyense mwa anthuŵa adyeko ngakhale pang'ono.” Wophunzira wake wina, dzina lake Andrea, mbale wake wa Simoni Petro, adauza Yesu kuti, “Pali mnyamata pano, ali ndi buledi msanu wabarele, ndi tinsomba tiŵiri. Koma zimenezi zingachitenji kwa anthu onseŵa?” Yesu adati, “Auzeni anthu akhale pansi.” (Pamenepo panali msipu wambiri.) Anthuwo adakhaladi pansi. Amuna okha analipo ngati zikwi zisanu. Tsono Yesu adatenga buledi uja, ndipo atayamika Mulungu, adagaŵira anthu amene adaakhala pansiwo. Adateronso ndi tinsomba tija, naŵagaŵira monga momwe anthuwo ankafunira. Anthu onsewo atakhuta, Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Tolani zotsala kuti pasatayikepo kanthu.” Adatoladi zotsala zonse za buledi msanu uja, nadzaza madengu khumi ndi aŵiri. Pamene anthu aja adaona chizindikiro chozizwitsa chimene Yesu adachitacho, adati, “Zoonadi ameneyu ndi Mneneri uja amene ankanena kuti adzabwera pansi panoyu.” Yesu adaadziŵa kuti anthuwo ankati adzamgwire ndi kumlonga ufumu. Motero adaŵachokera nakakweranso m'phiri payekha. M'mene kunkayamba kuda, ophunzira ake a Yesu adatsikira ku nyanja. Kumeneko adaloŵa m'chombo, nayamba kuwoloka nyanja kupita ku Kapernao. Mdima udagwa, Yesu osafikabe kwa iwo. Komanso nyanja idaavwanduka, chifukwa mphepo inkaomba kwambiri. Atapalasa chombo ulendo wokwanira mitunda itatu kapena inai, adaona Yesu akuyenda pa madzi nkumayandikira ku chombo chao, motero iwowo adachita mantha. Koma Yesu adati, “Ndine, musaope.” Adamkweza Yesu m'chombomo mokondwa, ndipo nthaŵi yomweyo chombocho chidakocheza kumtunda kumene adaalingako. M'maŵa mwake khamu la anthu limene lidaatsalira ku tsidya lija la nyanja, lidaadziŵa kuti chombo chinalipo chimodzi chokha. Anthuwo adaadziŵanso kuti Yesu sadaloŵe m'chombomo pamodzi ndi ophunzira ake, koma kuti ophunzira akewo anali atapita okha. Komabe zombo zina zochokera ku Tiberiasi zidafika pafupi ndi malo amene anthu aja adaadyera chakudya Ambuye atayamika Mulungu. Khamu lija lidaona kuti Yesu kulibe, ophunzira ake omwe kulibenso. Tsono anthu onsewo adaloŵa m'zombo zija, napita ku Kapernao kunka nafunafuna Yesu. Pamene anthu aja adampeza Yesu kutsidya kwa nyanja, adamufunsa kuti, “Aphunzitsi, mudafika liti kuno?” Yesu adati, “Kunena zoona, inu mukundifuna osati chifukwa mudazimvetsa zizindikiro zozizwitsa zija ai, koma chifukwa mudadya chakudya chija mpaka kukhuta. Musamagwira ntchito kuti mungopeza chakudya chimene chimaonongeka, koma muzigwira ntchito kuti mupeze chakudya chokhalitsa, chimene chili cha moyo wosatha. Mwana wa Munthu ndiye adzakupatsani chakudya chimenechi, pakuti Mulungu Atate adamuvomereza motsimikiza.” Pamenepo anthu aja adayamba kufunsana kuti, “Titanitu tsono kuti titsate bwino zimene Mulungu afuna?” Yesu adaŵayankha kuti, “Chimene Mulungu afuna kuti muchite nchakuti mundikhulupirire Ineyo amene Mulungu adandituma.” Iwo adafunsanso kuti, “Mungatiwonetse chizindikiro chotani kuti tikachiwona tikukhulupirireni? Nanga muchitapo chiyani? Makolo athu ankadya mana m'chipululu muja, monga Malembo akunenera kuti, ‘Ankaŵapatsa chakudya chochokera Kumwamba kuti adye.’ ” Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti amene ankakupatsani chakudya chochokera Kumwambacho, si Mose ai. Atate anga ndiwo amene amakupatsani chakudya chenicheni chochokera Kumwamba. Pakuti chakudya chimene Mulungu amapereka, ndicho chimene chimatsika kuchokera Kumwamba, ndipo chimapereka moyo kwa anthu a pa dziko lonse lapansi.” Apo anthuwo adapempha Yesu kuti, “Ambuye, muzitipatsa chakudya chimenecho masiku onse.” Yesu adaŵauza kuti, “Chakudya chopatsa moyocho ndine. Munthu aliyense wodza kwa Ine, sadzamva njala. Ndipo aliyense wokhulupirira Ine, sadzamva ludzu konse. “Ndidakuuzani kuti inde inu mwandiwona, komabe simukhulupirira. Onse amene Atate andipatsa, adzabwera kwa Ine. Ndipo munthu aliyense wodza kwa Ine, sindidzamkana konse. Pajatu ndidatsika kuchokera Kumwamba kudzachita zofuna za Iye amene adandituma, osati kuti ndidzachite zofuna Ine ai. Ndipo chofuna Iye amene adandituma nchakuti ndisatayepo ndi mmodzi yemwe mwa amene Iye adandipatsa, koma onse ndidzaŵaukitse kwa akufa pa tsiku lomaliza. Pakuti chimene Atate anga afuna nchakuti munthu aliyense amene aona Mwanayo namkhulupirira, akhale ndi moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.” Pamenepo Ayudawo adayamba kung'ung'udza chifukwa Yesu adaati, “Ine ndine chakudya chotsika kuchokera Kumwamba.” Iwo ankanena kuti, “Kodi ameneyu si Yesu, mwana wa Yosefe uja? Bambo wake ndi mai wake suja tikuŵadziŵa? Nanga tsono anganene bwanji kuti, ‘Ndidatsika kuchokera Kumwamba?’ ” Yesu adaŵayankha kuti, “Musang'ung'udze inu. Palibe munthu amene angabwere kwa Ine, ngati Atate amene adandituma samkoka. Ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza. Paja aneneri adalemba kuti, ‘Onse adzakhala ophunzitsidwa ndi Mulungu.’ Munthu aliyense womva Atate, nkuphunzira kwa Iwo, amadza kwa Ine. Sindiye kutitu wina aliyense adaona Atate ai, koma Ine ndekha amene ndidachokera kwa Mulungu; Ineyo ndi amene ndidaona Atate. “Ndithu ndikunenetsa kuti wokhulupirira Ine, ali nawo moyo wosatha. Ine ndine chakudya chopatsa moyo. Makolo anu ankadya mana m'chipululu muja, komabe adafa. Koma chakudya chimene ndikunenachi ndi chimene chidatsika kuchokera Kumwamba, kuti munthu atachidya asafe. Ine ndine chakudya chamoyo chimene chidatsika kuchokera Kumwamba. Munthu wodya chakudyachi, adzakhala ndi moyo mpaka muyaya. Ndipo chakudyacho chimene Ine ndidzapereka ndi thupi langa, limene ndikulipereka kuti anthu a pa dziko lonse lapansi akhale ndi moyo.” Pamenepo Ayuda aja adayamba kukangana okhaokha, ankati, “Munthu ameneyu angathe bwanji kutipatsa thupi lake kuti tidye?” Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti ngati simudya thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa magazi ake, simungakhale ndi moyo mwa inu. Aliyense wodya thupi langa ndi kumwa magazi anga, ali ndi moyo wosatha, ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza. Pakuti thupi langa ndi chakudya chenicheni, ndipo magazi anga ndi chakumwa chenicheni. Aliyense wodya thupi langa ndi kumwa magazi anga amakhala mwa Ine, ndipo Ine ndimakhala mwa iyeyo. Monga Atate amoyo adandituma, ndipo Ine ndili ndi moyo pokhala mwa Iwo, momwemonso aliyense wodya Ine, adzakhala ndi moyo pokhala mwa Ine. Chakudya chimene chidatsika kuchokera Kumwamba nchimenechi. Nchosiyana ndi mana aja amene makolo anu ankadya koma nkufabe. Wodya chakudya chimenechi, adzakhala ndi moyo mpaka muyaya.” Yesu adanena zimenezi pamene ankaphunzitsa m'nyumba yamapemphero ya ku Kapernao. Ophunzira ambiri a Yesu atamva zimenezi adati, “Mau ameneŵa ngapatali. Angathe kuŵavomera ndani?” Yesu adaadziŵa mumtima mwake kuti ophunzira ake akung'ung'udza za zimenezi. Tsono adaŵafunsa kuti, “Kodi zimenezi mukukhumudwa nazo? Nanga mudzatani mukadzaona Mwana wa Munthu akukwera kunka kumene anali kale? Mzimu wa Mulungu ndiwo umapatsa moyo, mphamvu ya munthu siipindula konse. Mau amene ndalankhula nanu ndiwo amapatsa mzimu wa Mulungu ndiponso moyo. Koma pali ena mwa inu amene sakukhulupirira.” (Pakuti Yesu adaadziŵiratu mpachiyambi pomwe amene sadzakhulupirira, adaamudziŵiratunso amene analikudzampereka kwa adani ake.) Tsono adati, “Nchifukwa chake ndinakuuzani kuti palibe munthu amene angabwere kwa Ine ngati Atate sampatsa mphamvu zobwerera kwa Ine.” Kuchokera pamenepo ophunzira ambiri a Yesu adamsiya, osayenda nayenso. Tsono Yesu adafunsa ophunzira khumi ndi aŵiri aja kuti, “Nanga inu, kodi inunso mukufuna kuchoka?” Simoni Petro adati “Ambuye, nanga tingapitenso kwa yani? Muli nawo ndinu mau opatsa moyo wosatha. Ife ndiye tikukhulupirira ndipo tikudziŵa kuti ndinu Woyera uja wochokera kwa Mulungu.” Apo Yesu adati, “Paja ndidakusankhani inu khumi ndi aŵiri, si choncho? Komabe mmodzi mwa inu ndi Satana?” Ankanena Yudasi, mwana wa Simoni Iskariote. Ngakhale anali mmodzi mwa ophunzira aja khumi ndi aŵiri, koma ndiye amene analikudzapereka Yesu kwa adani ake. Pambuyo pake Yesu ankayendera dera la Galileya. Sadafune kukayendera dera la Yudeya, chifukwa akuluakulu a Ayuda ankafuna kumupha. Nthaŵiyo nkuti chikondwerero cha Misasa chili pafupi. Tsono abale ake a Yesu adamuuza kuti, “Bwanji muchokeko kuno, mupite ku Yudeya kuti ophunzira anu kumeneko nawonso akaone ntchito zamphamvu zimene mukuchitazi. Munthu sachita kanthu m'seri akafuna kudziŵika ndi anthu. Popeza kuti Inu mukuchita ntchito zoterezi, mudziwonetse poyera pamaso pa anthu onse.” (Ndiye kuti abale akewo ankatero chifukwa ngakhale iwo omwe sankamukhulupirira.) Yesu adaŵauza kuti, “Nthaŵi yanga siinafikebe, koma yanu ndi nthaŵi iliyonse. Anthu ongokonda zapansipano sangadane nanu, koma amadana ndi Ine, chifukwa ndimapereka umboni wosonyeza kuti ntchito zao nzoipa. Inuyo pitani kuchikondwereroko. Ine sindipitako ku chikondwerero chimenechi, chifukwa nthaŵi yanga yoyenera siinafike.” Yesu atanena zimenezo, adatsalira m'Galileya. Koma abale ake atapita ku chikondwerero cha Misasa chija, Yesu nayenso adapitako. Sadapite moonekera, koma mobisika. Akulu a Ayuda ankamufunafuna kuchikondwereroko, nkumafunsana kuti, “Kodi amene uja ali kuti?” Ndipo panali manong'onong'o ambiri okamba za Iye pakati pa khamu la anthu. Ena ankanena kuti, “Ndi munthutu wabwino.” Koma ena ankati, “Iyai, amangosokeza anthu ameneyu.” Komabe panalibe munthu wolankhula poyera za Iye, chifukwa choopa akulu a Ayuda. Chikondwerero chija chikali pakati, Yesu adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu nayamba kuphunzitsa. Akulu a Ayuda adadabwa nati, “Bwanji munthu ameneyu ali ndi nzeru zotere, pamene sadaphunzire konse?” Yesu adati, “Zimene ndimaphunzitsa si zangatu ai, ndi za Atate amene adandituma. Aliyense wofuna kuchita kufuna kwa Mulungu, adzadziŵa ngati zimene Ine ndimalankhula nzochokera kwa Mulungu kapena kwa Ine ndekha. Amene amangolankhula zakezake, amadzifunira yekha ulemu. Koma yemwe amafunira ulemu amene adamtuma, ameneyo ndiye woona, ndipo mumtima mwake mulibe chinyengo. Kodi suja Mose adakupatsani Malamulo a Mulungu? Komabe palibe ndi mmodzi yemwe mwa inu amene akuŵatsata. Nanga mukufuniranji kundipha?” Koma khamu la anthu lidamuyankha kuti, “Wagwidwa ndi mizimu yoipa Iwe. Akufuna kukupha ndani?” Yesu adati, “Ndinangochita ntchito yozizwitsa imodzi yokha, nonsenu nkumadabwa. Mose adakulamulani kuti muziwumbala ana anu aamuna (ngakhale mwambowo si wochokera kwa Mose koma kwa makolo); ndipo inu mumaumbala mwana wamwamuna ngakhale mpa tsiku la Sabata. Mwanayo mumamuumbala pa Sabata, kuwopa kuti Lamulo la Mose lingaphwanyidwe. Bwanji mukuipidwa nane chifukwa ndinachiritsa munthu kwathunthu pa tsiku la Sabata? Musamaweruza poyang'ana maonekedwe chabe, koma muziweruza molungama.” Pamenepo anthu ena a ku Yerusalemu adati, “Kodi munthu akufuna kumupha uja, si ameneyu? Si uyu akulankhula poyerayu, popandanso wonenapo kanthu! Kodi kapenatu ndiye kuti akuluakulu akuzindikiradi kuti ameneyu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja eti? Komatu Mpulumutsi wolonjezedwa uja akadzabwera, palibe amene adzadziŵe kumene wachokera. Koma uyu tonse tikudziŵa kumene adachokera.” Pamene Yesu ankaphunzitsa m'Nyumba ya Mulungu, adalankhula mokweza mau kuti, “Ine mukundidziŵa, ndipo kumene ndidachokera mukudziŵakonso. Koma sindidabwere mwa kufuna kwanga ai. Atate amene ali wokhulupirika ndiwo adandituma. Inu simukuŵadziŵa. Koma Ine ndikuŵadziŵa, chifukwa ndine wochokera kwa Iwo, ndipo ndiwo adandituma.” Pamenepo anthu adafuna kumgwira Yesu, koma panalibe ndi mmodzi yemwe amene adamkhudza, chifukwa nthaŵi yake inali isanafike. Koma anthu ambiri a m'khamu limenelo adamkhulupirira, ndipo ankati, “Kodi akadzabwera Mpulumutsi wolonjezedwa uja, adzachita zizindikiro zozizwitsa zoposa zimene munthuyu wachita?” Afarisi adamva manong'onong'o a chikhamu cha anthu okamba za Yesu. Tsono iwo pamodzi ndi akulu a ansembe adatuma asilikali a ku Nyumba ya Mulungu kuti akamgwire. Apo Yesu adati, “Ndili nanube kanthaŵi pang'ono ndisanapite kwa Atate amene adandituma. Mudzandifunafuna, koma simudzandipeza. Ndipo kumene ndizikakhala Ine, inu simungathe kufikako.” Pamenepo akulu a Ayudawo adayamba kufunsana kuti, “Kodi iyeyu afuna kupita kuti kumene ife sitingakampeze? Kodi kapena akufuna kupita kwa anzathu amene adabalalikira kwa anthu a mitundu ina? Monga nkuti afuna kukaphunzitsa anthu akunja? Akunena kuti, ‘Mudzandifunafuna koma simudzandipeza,’ ndiponso kuti, ‘Kumene ndizikakhala Ine, inu simungakafikeko.’ Kodi mau ameneŵa akutanthauza chiyani?” Tsiku lotsiriza la chikondwerero chija linali lalikulu. Pa tsikulo Yesu adaimirira nkunena mokweza kuti, “Ngati pali munthu ali ndi ludzu, abwere kwa Ine kuti adzamwe. Paja Malembo akuti, ‘Munthu wokhulupirira Ine, mtima wake udzakhala ngati gwelo la mitsinje ya madzi opatsa moyo.’ ” (Pakutero Yesu ankanena za Mzimu Woyera amene anthu okhulupirira Iye analikudzalandira. Nthaŵi imeneyo nkuti Mzimu Woyera asanafike, chifukwa Yesu anali asanalandire ulemerero wake.) Pamene khamu la anthu lidamva mau ameneŵa, ena mwa iwo ankati, “Zoonadi munthuyu ndiye Mneneri uja.” Ena ankanena kuti, “Ameneyu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja.” Koma ena ankanena kuti, “Kodi Mpulumutsiyo nkuchokera ku Galileya ngati? Suja Malembo akuti kholo lake ndi mfumu Davide? Ndipo sujanso akuti adzachokera ku mudzi wa Betelehemu kumene Davideyo anali?” Choncho khamu la anthu lidagaŵikana chifukwa cha Iye. Ena ankafuna kumgwira, koma panalibe amene adamkhudza. Asilikali a ku Nyumba ya Mulungu aja adabwerera kwa akulu a ansembe ndi kwa Afarisi aja. Iwo adafunsa asilikaliwo kuti, “Bwanji simudabwere naye?” Asilikali aja adayankha kuti, “Palibenso wina amene adalankhulapo ngati munthu ameneyo nkale lonse.” Apo Afarisi adati, “Kani inunso wakunyengani? Kodi mudamvapo kuti pakati pa akuluakulu kapena pakati pa Afarisi alipo wokhulupirira amene uja? Koma anthu wambaŵa sadziŵa Malamulo a Mose; ngotembereredwa basi!” Tsono Nikodemo, mmodzi mwa Afarisi, yemwe uja amene kale adaapita kwa Yesu, adafunsa anzakewo kuti, “Kodi Malamulo athu amatilola kuweruza munthu tisanamve mau ake kuti tidziŵe zimene wachita?” Iwo adati, “Kani iwenso ndiwe wa ku Galileya? Kafunefune m'Malembo ndipo udzaona kuti palibe mneneri wochokera ku Galileya.” [ Pamenepo anthu onse adabwerera kwao.] [Koma Yesu adapita ku Phiri la Olivi. M'mamaŵa adabweranso ku Nyumba ya Mulungu. Anthu onse adadza kwa Iye, Iyeyo nkukhala pansi nayamba kuŵaphunzitsa. Aphunzitsi a Malamulo pamodzi ndi Afarisi adabwera ndi mai amene adaamugwira akuchita chigololo, nkumukhalitsa pakati pao. Tsono adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, mai uyu wagwidwa ali m'kati mochita chigololo. Paja m'buku la Malamulo Mose adatilamula kuti munthu wotere tizipha pakumponya miyala. Nanga Inuyo mukuti chiyani pamenepa?” Adaamufunsa funsoli kuti amuyese ndi kumpeza chifukwa. Koma Yesu adaŵerama, nayamba kulemba pansi ndi chala chake. Popeza kuti iwo adaapitirirabe kumufunsa, Yesu adaŵeramuka naŵauza kuti, “Pakati panupa amene sadachimwepo konse, ayambe ndiye kumponya mwala maiyu.” Atatero, adaŵeramanso namalemba pansi. Koma iwo atamva zimenezi, adayamba kuchokapo mmodzimmodzi, kuyambira akuluakulu; Yesu nkutsalira yekha, mai uja ali chikhalire pakati pompaja. Kenaka Yesu adaŵeramuka namufunsa kuti, “Kodi mai, ali kuti anthu aja? Kodi palibe ndi mmodzi yemwe amene wakuzengani mlandu?” Maiyo adati, “Inde Ambuye, palibe.” Tsono Yesu adamuuza kuti, “Inenso sindikukuzengani mlandu. Pitani koma kuyambira tsopano musakachimwenso.”] Pambuyo pake Yesu adalankhulanso ndi Afarisi aja, adati, “Ine ndine kuŵala kounikira anthu onse. Munthu wotsata Ine, sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuŵala kotsogolera anthu ku moyo.” Apo Afarisi adamuuza kuti, “Ukudzichitira wekha umboni. Umboni wakowo ngwosakwanira.” Yesu adati, “Ngakhale ndikudzichitira ndekha umboni, komabe umboni wangawo ngwoona, pakuti ndikudziŵa kumene ndidachokera, ndiponso kumene ndikupita. Koma inu simukudziŵa kumene ndidachokera, kapenanso kumene ndikupita. Inu mumaweruza potsata maganizo a anthu chabe. Ine sindiweruza munthu aliyense. Koma ndikati ndiweruze, ndimaweruza molungama, pakuti sindili ndekha ai, palinso Atate amene adandituma. Ndipo m'Malamulo anu mudalembedwa kuti umboni wa anthu aŵiri ngwokwanira. Ine ndimadzichitira ndekha umboni, nawonso Atate amene adandituma amandichitira umboni.” Apo iwo adamufunsa kuti, “Atate akowo ali kuti?” Yesu adati, “Ine simundidziŵa, Atate anganso simuŵadziŵa. Mukadandidziŵa, bwenzi mutaŵadziŵanso Atate anga.” Yesu adanena mau ameneŵa pamene ankaphunzitsa m'Nyumba ya Mulungu, m'chipinda cholandiriramo zopereka za anthu. Panalibe amene adamgwira, chifukwa nthaŵi yake inali isanafike. Pambuyo pake Yesu adaŵauzanso kuti, “Ine ndikupita. Mudzandifunafuna koma mudzafera m'machimo anu. Kumene ndikupita Ine, inu simungathe kufikako.” Apo Ayuda adati, “Kodi kapena akufuna kukadzipha, umo akunena kuti, ‘Kumene ndikupita Ine, inu simungathe kufikako?’ ” Yesu adaŵauza kuti, “Inu ndinu ochokera pansi pano, Ine ndine wochokera Kumwamba. Inu ndinu a dziko lino lapansi, Ine sindine wa dziko lino lapansi ai. Nchifukwa chake ndakuuzani kuti mudzafera m'machimo anu. Pakuti ngati simukhulupirira kuti Ine ndine Ndilipo, mudzaferadi m'machimo anu.” Apo iwo adamufunsa kuti, “Iweyo ndiwe yani?” Yesu adati, “Nchomwe ndakhala ndikukuuzani chiyambire ndithu. Ndili ndi zambiri zoti ndinene za inu, ndiponso zoti ndikutsutsireni. Koma amene adandituma ngwoona, ndipo ndimauza anthu a pansi pano zimene Iyeyo adandiwuza.” Anthu aja sadazindikire kuti Yesu akunena za Atate. Tsono Yesu adaŵauza kuti, “Mukadzapachika Mwana wa Munthu, pamenepo mudzadziŵa kuti Ine ndine Ndilipo. Mudzadziŵanso kuti sindichita kanthu pandekha, ndimalankhula zimene Atate adandiphunzitsa. Ndipo amene adandituma, ali nane pamodzi. Iye sadandisiye ndekha, chifukwa nthaŵi zonse ndimachita zomkondweretsa.” Pamene Yesu ankalankhula zimenezi, anthu ambiri adamkhulupirira. Yesu adauza anthu amene adamkhulupirirawo kuti, “Ngati mumvera mau anga nthaŵi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga. Mudzadziŵa zoona zenizeni, ndipo zoonazo zidzakusandutsani aufulu.” Iwo adati, “Ife ndife ana a Abrahamu, ndipo chikhalire chathu sitinakhalepo akapolo a wina aliyense. Nanga bwanji ukuti, ‘Mudzasanduka aufulu?’ ” Yesu adaŵayankha kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti aliyense wochita tchimo ndi kapolo wa tchimolo. Kapolo sakhala nao m'banja nthaŵi zonse, koma mwana. Tsono ngati Mwana akumasulani, mudzakhaladi mfulu. Ndikudziŵa kuti ndinu ana a Abrahamu, komabe mukufuna kundipha, chifukwa simukuvomereza mau anga m'mitima mwanu. Ine ndimalankhula zimene ndidaziwona kwa Atate anga, koma inu mumachita zimene mudamva kwa atate anu.” Iwo adati, “Ifetu atate athu ndi Abrahamu.” Yesu adaŵauza kuti, “Mukadakhala ana a Abrahamu, bwenzi mukuchita zimene Abrahamuyo ankachita. Koma tsopano mukufuna kundipha Ine, amene ndakuuzani zoona zimene ndidamva kwa Mulungu. Abrahamu sadachite zotere. Inu mukuchita zimene tate wanu amachita.” Iwo adamuuza kuti, “Ife ndiye sindife ana am'chigololotu ai. Tili ndi Tate mmodzi yekha, ndiye Mulungu.” Yesu adati, “Mulungu akadakhaladi Atate anu, bwenzi mutandikonda Ine, chifukwa ndidafumira kwa Mulungu, ndipo tsopano ndili kuno. Sindidabwere ndi ulamuliro wa Ine ndekha ai, koma Iyeyo adachita kundituma. Nanga chifukwa chiyani simukumvetsa zimene ndikunena? Chifukwa chake nchakuti simungakonde konse kumva mau anga. Inu ndinu ana a Satana. Iye ndiye tate wanu, ndipo mukufuna kumachita zimene tate wanuyo amalakalaka. Iye uja chikhalire ngwopha anthu. Sadakhazikike m'zoona, chifukwa mwa iye mulibe zoona. Kunena bodza ndiye khalidwe lake, pakuti ngwabodza, nkukhalanso chimake cha mabodza onse. Koma Ine ndimalankhula zoona, nchifukwa chake simundikhulupirira. Kodi ndani mwa inu anganditsimikize kuti ndine wochimwa? Nanga ngati ndikunena zoona, mukulekeranji kundikhulupirira? Munthu wochokera kwa Mulungu amatchera khutu ku mau a Mulungu. Koma inu simuchokera kwa Mulungu ai, nchifukwa chake simutchera khutu.” Ayuda aja pomuyankha Yesu, adati, “Kodi ife sitikunena zoona kuti Iwe ndiwe Msamariya, ndipo kuti ndiwe wogwidwa ndi mizimu yoipa?” Yesu adati, “Ine sindidagwidwe ndi mizimu yoipa. Ndimalemekeza Atate anga, koma inu mumandipeputsa. Komabe Ine sindidzifunira ndekha ulemu. Alipo wina wondifunira ulemu, ndiye amaweruza. Ndithu ndikunenetsa kuti munthu akamvera mau anga, sadzafa konse.” Ayudawo adamuuza kuti, “Tsopano tadziŵadi kuti ndiwe wogwidwa ndi mizimu yoipa. Abrahamu adamwalira, aneneri nawonso adamwalira. Ndiye Iwe ukuti, ‘Munthu akamvera mau anga sadzafa konse.’ Monga Iweyo nkupambana atate athu Abrahamu amene adamwalira? Anenerinso adamwalira. Kodi umadziyesa yani?” Yesu adati, “Ndikadzilemekeza ndekha, ulemu wangawo ngwachabe. Alipo ondilemekeza. Amenewo ndi Atate anga, omwe inuyo mumati ndi Mulungu wanu. Inu simudaŵadziŵe, koma Ine ndimaŵadziŵa, mwakuti ndikadati sindiŵadziŵa ndikadakhala wonama ngati inuyo. Koma ndimaŵadziŵa, ndipo ndimamvera mau ao. Atate anu Abrahamu adaasekera poyembekeza kuti adzaona tsiku la kubwera kwanga. Adaliwonadi nakondwa.” Apo Ayuda adamufunsa kuti, “Zaka zako sizinakwane ndi makumi asanu omwe, ndiye nkukhala utaona Abrahamu?” Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti Abrahamu asanabadwe, Ine ndilipo.” Pamenepo Ayuda aja adayamba kutola miyala kuti amlase. Koma Yesu adazemba natuluka m'Nyumba ya Mulunguyo. Pamene Yesu ankayenda, adaona munthu wa khungu lobadwa nalo. Ophunzira ake adamufunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi adachimwa ndani kuti munthu ameneyu abadwe wakhungu? Adachimwa ndi iyeyu kapena makolo ake?” Yesu adati, “Sikuti iyeyu adachimwa kapena makolo ake ai. Koma adabadwa wakhungu kuti Mulungu aonetse ntchito zake mwa iye. Kukali usana tizigwira ntchito za Atate amene adandituma. Usiku ukudza pamene munthu sangathe kugwira ntchito. Pamene ndili pansi pano, ndine kuŵala kounikira anthu onse.” Atanena zimenezi, Yesu adalavulira malovu pansi, nakanda thope ndi malovuwo. Kenaka adapaka thopelo m'maso mwa munthuyo, namuuza kuti, “Pita ukasambe ku dziŵe la Siloamu.” (Tanthauzo la Siloamu ndiye kuti, Wotumidwa.) Munthuyo adapitadi, adakasamba, nabwerako akupenya. Pamenepo anzake ndi anthu amene kale ankamuwona akupemphapempha adati, “Kodi uyu si uja ankakhala pansi apa nkumangopempha?” Ena adati, “Ndiye amene.” Ena nkumati, “Iyai, akungofanafana naye.” Koma mwiniwakeyo adati, “Ai ndithu, ndine amene.” Apo anthu aja adamufunsa kuti, “Nanga maso ako apenya bwanji?” Iyeyo adati, “Munthu uja amati Yesuyu anakanda thope nalipaka m'maso mwangamu. Kenaka anandiwuza kuti, ‘Pita, ukasambe ku Siloamu. Ndinapitadi, ndipo nditasamba, ndayamba kupenya.’ ” Anthuwo adamufunsa kuti, “Iyeyo ali kuti?” Munthu uja adati, “Kaya, sindikudziŵa.” Tsono munthu uja kale sankapenyayu adapita naye kwa Afarisi. Tsiku limene Yesu adaakanda thope namchiritsalo linali la Sabata. Tsono Afarisi nawonso adamufunsa munthu uja kuti, “Iwe, wapenya bwanji?” Iye adaŵauza kuti, “Anandipaka thope m'maso mwanga, ine nkukasamba, ndipo tsopano ndikupenya.” Afarisi ena adati, “Munthu amene uja ngwosachokera kwa Mulungu, chifukwa satsata lamulo lokhudza tsiku la Sabata.” Koma ena adati, “Kodi inu, munthu wochimwa nkuchita zizindikiro zozizwitsa zotere?” Choncho panali kutsutsana. Tsono Afarisi aja adamufunsanso munthu uja kale sankapenyayu, adati, “Kodi iweyo ukuti chiyani za Iyeyo, m'mene wakuchiritsamu?” Iye adati, “Ndi mneneritu basi.” Koma akulu a Ayudawo sadakhulupirire kuti munthuyo kale sankapenya ndipo tsopano akupenya, mpaka adaitanitsa makolo ake. Tsono adaŵafunsa kuti, “Kodi inu, uyu ndi mwana wanu? Ndiye mukuti adaabadwadi wosapenya? Nanga zatani kuti tsopano akupenya?” Makolo ake adati, “Chimene tikudziŵa ife nchakuti ameneyu ndi mwana wathu, ndipo adaabadwadi wosapenya. Koma kuti tsopano akupenya, sitikudziŵa m'mene zachitikira. Zoti wamupenyetsa ndani kaya, ife sitikudziŵanso. Mufunseni mwiniwakeyu, ngwamkulu, afotokoze yekha.” Makolo akewo adaatero chifukwa ankaopa akulu a Ayuda. Pakuti Ayuda anali atapangana kale kuti, ngati munthu adzavomereza kuti Yesu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja, adzamdula ku mpingo. Nchifukwa chake makolo akewo adati, “Ngwamkulu, mufunseni mwiniwakeyu.” Pamenepo Ayuda aja adamuitana kachiŵiri munthu uja kale sankapenyayu, namuuza kuti, “Lemekeza Mulungu, ndipo unene zoona. Ife tikudziŵa kuti munthu amene uja ngwochimwa.” Iye adati, “Zakuti Iye ngwochimwa, ine sindikudziŵa. Chinthu chimodzi chokha ndikudziŵa, kuti kale ndinali wosapenya, koma tsopano ndikupenya.” Iwo adamufunsa kuti, “Kodi anachita chiyani pamene anakupenyetsa?” Iye adati, “Ndakuuzani kale, koma simumasamalako. Nanga chifukwa chiyani mukufuna kuzimvanso? Kapenatu nanunso mukufuna kukhala ophunzira ake eti?” Pamenepo iwo adayamba kumlalatira, adati, “Wophunzira wake ndi iweyo. Ife ndifetu ophunzira a Mose. Tikudziŵa kuti Mulungu adalankhula ndi Mose, koma uyu sitikudziŵa kumene wachokera.” Munthuyo adati, “Pakudabwitsatu mpamenepa: kuti inuyo simukudziŵa kumene Iye wachokera, komabe wandipenyetsa. Timadziŵa kuti Mulungu samvera anthu ochimwa. Koma munthu akasamala za Mulungu, nachita zimene Mulungu afuna, Mulungu amamumvera. Nkale lomwe sikudamveke konse kuti wina adapenyetsa munthu wakhungu. Munthu ameneyu akadapanda kuchokera kwa Mulungu, sakadatha konse kuchita kanthu.” Iwo adati, “Iwe udabadwa m'machimo okhaokha. Ndiye iweyo nkutiphunzitsa ife?” Atatero adamtulutsa nkumudula ku mpingo. Yesu adamva kuti Ayuda amtulutsa ndi kumdula ku mpingo munthu uja. Tsono pamene adampeza, adamufunsa kuti, “Kodi ukukhulupirira Mwana wa Munthu?” Iye adati, “Ambuye, mundiwuzetu ndani Iyeyo, kuti ndimkhulupirire.” Yesu adamuuza kuti, “Wamuwona kale, ndi yemwe akulankhula nawe.” Iye adati, “Ambuye, ndikukhulupirira.” Atatero adamgwadira. Tsono Yesu adati, “Ndidabwera pansi pano kudzaweruza, kuti osapenya apenye, ndipo openya achite khungu.” Afarisi ena amene anali pafupi naye, atamva zimenezi adamufunsa kuti, “Kodi monga ifenso ndife akhungu?” Yesu adati, “Mukadakhala akhungu, bwenzi mulibe mlandu. Koma chifukwa mukuti, ‘Tikupenya,’ ndiye kuti mlandu wanu ulipobe.” “Kunena zoona, munthu woloŵa m'khola la nkhosa osadzera pa khomo, koma kuchita kukwerera pena, ameneyo ndi wakuba ndi wolanda. Koma munthu woloŵera pa khomo ndiye mbusa wa nkhosazo. Iyeyo mlonda amamtsekulira. Nkhosa zimamva mau ake, ndipo amaziitana maina nkhosa zakezo, nazitulutsa. Akazitulutsa nkhosa zake zonse, amazitsogolera, izo nkumamtsatira, chifukwa zimadziŵa mau ake. Mlendo sizidzamtsatira ai, zidzamthaŵa, chifukwa sizidziŵa mau a alendo.” Yesu adaŵaphera fanizoli, koma iwo sadamvetse zimene ankaŵauzazo. Tsono Yesu adatinso, “Ndithu ndikunenetsa kuti Ine ndine khomo la nkhosa. Ena onse amene adabwera Ine ndisanafike, ngakuba ndi olanda, koma nkhosa sizinaŵamvere. Khomo ndine. Munthu akaloŵera pa Ine, adzapulumuka. Azidzaloŵa ndi kutuluka, ndipo adzapeza chakudya. Wakuba amangodzera kuba, kupha ndi kuwononga. Koma Ine ndidabwera kuti nkhosazo zikhale ndi moyo, moyo wake wochuluka. “Ine ndine mbusa wabwino. Mbusa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa zake. Koma wolembedwa ntchito chabe akaona mmbulu ulikudza, amazisiya nkhosazo iye nkuthaŵa. Amatero popeza kuti si mbusa weniweni, ndipo nkhosa si zake ai. Tsono mmbulu uja umagwirapo zina, zina nkumwazikana. Wolembedwa ntchito uja amathaŵa, chifukwa amangotsata malipiro chabe, ndipo salabadirako za nkhosazo. Mbusa wabwino ndine. Nkhosa zanga ndimazidziŵa, ndipo izozo Ineyo zimandidziŵa, monga momwe Atate amadziŵira Ine, nanenso nkuŵadziŵa Atatewo. Ndimatayirapo moyo wanga pa nkhosazo. Ndili nazo nkhosa zina zimene sizili za m'khola lino. Zimenezonso ndiyenera kuzikusa. Zidzamva mau anga, ndipo padzakhala gulu limodzi mbusa wakenso mmodzi. “Nchifukwa chake Atate amandikonda, popeza kuti ndikupereka moyo wanga kuti ndikautengenso. Palibe munthu wondilanda moyo wangawu, koma ndikuupereka ndekha. Ndili nazo mphamvu zoutaya moyo wanga, ndili nazonso mphamvu zoutenganso. Udindo umenewu ndidaulandira kwa Atate anga.” Anthu adaayambanso kutsutsana okhaokha chifukwa cha mau ameneŵa. Ambiri mwa iwo ankati, “Ali ndi mizimu yoipa, ndipo wapenga. Bwanji mukumumveranso Iyeyu?” Koma ena ankati, “Mau ameneŵa si a munthu wogwidwa ndi mizimu yoipa. Kodi mizimu yoipa nkupenyetsa anthu akhungu?” Ku Yerusalemu kunali chikondwerero chokumbukira kuperekedwanso kwa Nyumba ya Mulungu. Inali nyengo yozizira. Yesu ankangodziyendera m'Nyumba ya Mulungu, m'khonde lotchedwa Khonde la Solomoni. Anthu adamzinga namufunsa kuti, “Kodi udzaleka liti kutikayikitsa? Ngati ndiwe Mpulumutsi wolonjezedwa uja, tiwuze momveka.” Yesu adati, “Ndidakuuzani kale, komabe simukhulupirira. Ntchito zimene ndimachita m'dzina la Atate anga, ndizo zimandichitira umboni. Koma inu simukhulupirira konse, chifukwa simuli a m'gulu la nkhosa zanga. Nkhosa zanga zimamva mau anga. Ine ndimazidziŵa, ndipo zimanditsatira. Ndimazipatsa moyo wosatha, ndipo sizidzatayika konse. Palibe munthu wodzazilanda m'manja mwanga. Atate anga amene adandipatsa nkhosazo amapambana onse, ndipo palibe amene angathe kuzilanda m'manja mwao. Ine ndi Atate ndife amodzi.” Anthuwo adatolanso miyala kuti amlase. Yesu adaŵafunsa kuti, “Ndakuwonetsani ntchito zabwino zambiri zimene Atate adandichititsa. Nanga mwa zimenezi ntchito imene mukuti mundiponyere miyala ndi iti?” Anthu aja adamuyankha kuti, “Sitikufuna kukuponya miyala chifukwa cha ntchito yabwino ai, koma chifukwa ukunyoza Mulungu. Iwe, amene uli munthu chabe, ukudziyesa Mulungu.” Yesu adati, “Kodi m'Malamulo mwanu suja mudalembedwa kuti ‘Mulungu adati, Ndinu milungu?’ Paja mau a m'Malembo ngoona mpaka muyaya, ndipo Mwiniwakeyo adaŵatcha milungu anthu aja Iye ankalankhula nawoŵa. Inetu Atate adandipatula nandituma pansi pano. Tsono inuyo munganene bwanji kuti ndikunyoza Mulungu, chifukwa ndati ndine Mwana wa Mulungu? Ngati sindichita ntchito zimene Atate anga adandipatsa, musandikhulupirire. Koma ngati ndimazichitadi, khulupirirani ntchitozo, ngakhale simukhulupirira Ine. Apo mudzadziŵa mosapeneka konse kuti Atate amakhala mwa Ine, ndipo Ine ndimakhala mwa Atate.” Pamenepo anthu aja adafunanso kumgwira, koma Iye adazemba. Yesu adabwereranso kutsidya kwa mtsinje wa Yordani, kumene Yohane ankabatizira anthu poyamba paja, ndipo adakhala komweko. Anthu ambiri adadza kwa Iye, nkumanena kuti, “Yohane sadachite chizindikiro chozizwitsa ai, koma zonse zimene ankanena za Munthuyu zinali zoonadi.” Motero anthu ambiri adakhulupirira Yesu kumeneko. Panali munthu wina, dzina lake Lazaro, amene ankadwala. Anali wa ku mudzi wa Betaniya, kwao kwa Maria ndi mbale wake Marita. Mariayo ndi yemwe uja amene adaadzoza Ambuye ndi mafuta onunkhira, nkupukuta mapazi ao ndi tsitsi lake. Lazaro ankadwalayo anali mlongo wake. Tsono alongo ake aja adatumiza thenga kwa Yesu kukamuuza kuti, “Ambuye, bwenzi lanu uja akudwala.” Pamene Yesu adamva zimenezi adati, “Kudwalako safa nako ai, koma zatero kuti Mulungu alemekezedwe, ndipo kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe chifukwa cha matendawo.” Ndiye kuti Yesu ankakonda Marita ndi mng'ono wake Maria ndiponso Lazaro. Komabe pamene adamva za matendawo, Yesu adaswera masiku aŵiri pamalo pomwe adaaliripo. Pambuyo pake adauza ophunzira ake kuti, “Tiyeni tipitenso ku Yudeya.” Ophunzira akewo adati, “Aphunzitsi, tsopano apa Ayuda ankafuna kukuponyani miyala, ndiye mukuti mupitenso komweko?” Yesu adati, “Kodi suja usana uli ndi maora khumi ndi aŵiri? Munthu akayenda masana, sakhumudwa, chifukwa amaona kuŵala kwa dzikoku. Koma akayenda usiku, amakhumudwa chifukwa kuŵalako alibe.” Atatero adaŵauza kuti, “Lazaro, bwenzi lathu, wagona tulo, koma ndipita kuti ndikamdzutse ku tulo taketo.” Apo ophunzira ake adati, “Ambuye, ngati wagona tulo, achira.” Iwo ankayesa kuti akunena za tulo teniteni, koma Yesu ankanena za imfa yake ya Lazaro. Tsono Yesu adaŵauza mosabisa kuti, “Lazaro wamwalira, komabe chifukwa cha inu ndikukondwera kuti Ine kunalibe kumeneko, kuti choncho mukakhulupirire. Tiyeni tipiteko.” Pamenepo Tomasi, wotchedwa Didimo, adauza ophunzira anzake kuti, “Tiyeni ifenso tipite nao kuti tikafe naye pamodzi.” Pamene Yesu adafika ku Betaniya, adapeza Lazaro atagona m'manda masiku anai. Ku Betaniya kunali kufupi ndi ku Yerusalemu, mtunda wokwanira pafupi makilomita atatu. Panali anthu ambiri amene adaabwera kwa Marita ndi Maria kudzaŵapepesa chifukwa cha imfa ya mlongo wao. Pamene Marita adamva kuti Yesu akubwera, adapita kukamchingamira. Koma Maria adaatsalira m'nyumba. Tsono Marita adauza Yesu kuti, “Ambuye, mukadakhala kuno, sibwenzi mlongo wanga atamwalira. Koma ngakhale tsopano, ndikudziŵa kuti Mulungu adzakupatsani zilizonse mungampemphe.” Yesu adamuuza kuti, “Mlongo wako adzauka.” Marita adati, “Ndikudziŵa kuti adzauka podzauka anthu kwa akufa pa tsiku lomaliza.” Yesu adamuuza kuti, “Woukitsa anthu kwa akufa ndiponso woŵapatsa moyo ndine. Munthu wokhulupirira Ine, ngakhale afe adzakhala ndi moyo. Ndipo aliyense amene ali ndi moyo nakhulupirira Ine, sadzafa konse. Kodi ukukhulupirira zimenezi?” Iye adati, “Inde Ambuye, ndikukhulupirira kuti Inu ndinu Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu, amene adayenera kubwera pansi pano.” Marita atanena zimenezi, adaitanira paseri Maria mng'ono wake namuuza kuti, “Afika Aphunzitsi, akukuitana.” Maria atamva zimenezi, adanyamuka msangamsanga, nadza kwa Yesu. Pamenepo nkuti Yesu asanafike kumudziko, koma anali chikhalire pamalo pomwe Marita adaakumana naye. Anthu amene anali m'nyumba akupepesa Mariayo, ataona kuti wanyamuka msangamsanga ndi kutuluka, adamtsatira. Ankayesa kuti akupita kumanda kukalira kumeneko. Maria atafika pamene panali Yesu, namuwona, adadzigwetsa kumapazi kwake nati, “Ambuye, mukadakhala kuno, sibwenzi mlongo wanga atamwalira.” Yesu ataona Maria akulira, ndiponso anthu amene adaadza naye iwonso akulira, zidamkhudza kwambiri ndipo adavutika mu mtima. Tsono adaŵafunsa kuti, “Mudamuika kuti?” Iwo adati, “Ambuye, tiyeni mukaone.” Yesu adayamba kulira. Pamenepo anthu aja adati, “Onani, ankamukonda zedi.” Koma ena mwa iwo adati, “Munthu uyu suja adapenyetsa munthu wosapenya uja? Monga sakadatha kuchitapo kanthu kuti Lazaroyu asafe?” Yesu adavutikanso mu mtima, nakafika ku manda amene anali phanga. Pakhomo pake panali chimwala. Tsono adati, “Tachotsani chimwalacho.” Marita, mlongo wa womwalirayo, adamuuza kuti, “Pepani Ambuye, wayamba kale kununkha, pakuti wagonamo masiku anai.” Yesu adamufunsa kuti, “Kodi sindidakuuze kuti ukakhulupirira uwona ulemerero wa Mulungu?” Tsono anthu adachotsa chimwala chija. Yesu adayang'ana kumwamba nati, “Atate, ndikukuyamikani kuti mwandimvera. Ndikudziŵa kuti mumandimvera nthaŵi zonse. Koma ndanena zimenezi chifukwa cha khamu la anthu amene ali panoŵa, kuti akhulupirire kuti ndinu mudandituma.” Atatero adaitana mokweza mau kuti, “Lazaro, tuluka!” Pomwepo munthu amene adaamwalirayo adatuluka, miyendo yake ndi manja ake zili zomangidwa ndi nsalu zamaliro. Nkhope yake inali yokutidwa ndi nsalu. Yesu adaŵauza kuti, “Mmasuleni, ndipo mlekeni azipita.” Ambiri mwa anthu amene adaabwera kwa Maria, adaona zimene Yesu adaachita, ndipo adamkhulupirira. Koma ena adapita kwa Afarisi, nakaŵasimbira zimene Yesu adaachita. Apo akulu a ansembe ndi Afarisi adaitanitsa Bungwe Lalikulu la Ayuda, nafunsana kuti, “Titani pamenepa, popeza kuti munthuyu akuchita zozizwitsa zambiri? Tikamlekerera chomwechi, anthu onse adzamkhulupirira, ndipo Aroma adzabwera nkudzatiwonongera malo athu oyeraŵa ndiponso mtundu wathuwu.” Koma mmodzi mwa iwo, dzina lake Kayafa, amene anali mkulu wa ansembe onse chaka chimenecho, adaŵauza kuti, “Inu simudziŵa kanthu konse ai. Monga inu simukuwona kuti nkwabwino koposa kwa inu kuti munthu mmodzi afere anthu onse, m'malo moti mtundu wathu wonse uwonongeke?” (Kwenikwenitu sadanene zimenezi ndi nzeru za iye yekha ai. Koma popeza kuti anali mkulu wa ansembe onse chaka chimenecho, ankalosa kuti Yesu adzafera mtundu wa Ayuda. Tsono osati kungofera fuko chabe, komanso kusonkhanitsa pamodzi ana a Mulungu amene adabalalika.) Kuyambira tsiku limenelo akulu aja a Ayuda adayamba kupangana zoti amuphe. Nchifukwa chake Yesu sankayenda poyera pakati pa anthu. Koma adachokako napita ku dziko limene linali pafupi ndi chipululu, ku mudzi wina dzina lake Efuremu, ndipo adakhala kumeneko pamodzi ndi ophunzira ake. Chikondwerero cha Paska chija chinkayandikira. Choncho anthu ambiri ochokera ku midzi adapita ku Yerusalemu kukachita mwambo wa kudziyeretsa, Paska isanayambe. Ankamufunafuna Yesu, ndipo pamene adasonkhana m'Nyumba ya Mulungu ankafunsana kuti, “Kodi inu mukuganiza bwanji? Kodi monga Iye uja abwera kuchikondwerero kuno?” Koma akulu a ansembe ndi Afarisi anali atalamula kuti aliyense akadziŵa kumene kuli Yesu, aŵadziŵitse, kuti akamgwire. Atatsala masiku asanu ndi limodzi kuti chifike chikondwerero cha Paska, Yesu adadza ku Betaniya, kumene kunali Lazaro uja amene Iye adamuukitsa kwa akufa. Adamkonzera Yesu chakudya kumeneko, ndipo Marita ankaŵatumikira. Lazaro anali mmodzi mwa amene ankadya naye pamodzi. Tsono Maria adatenga mafuta onunkhira zedi a narido weniweni, amtengowapatali, okwanira theka la lita, nayamba kudzoza mapazi a Yesu, nkumaŵapukuta ndi tsitsi lake. M'nyumba monsemo mumvekere guu ndi fungo la mafutawo. Koma Yudasi Iskariote, mmodzi mwa ophunzira a Yesu, amene analikudzampereka kwa adani ake, adati, “Kodi bwanji mafuta ameneŵa sadaŵagulitse ndalama mazana atatu kenaka ndalamazo nkukapatsa anthu osauka?” Adaatero osati chifukwa chodera nkhaŵa osaukawo, koma chifukwa anali mbala. Iye ankasunga thumba la ndalama, nkumabamo. Yesu adati, “Mlekeni, mafutaŵa aŵasungire tsiku lodzaika maliro anga. Pajatu osauka muli nawo nthaŵi zonse, koma Ine simudzakhala nane nthaŵi zonse.” Anthu ambirimbiri atamva kuti Yesu ali ku Betaniya, adapita komweko. Sadapiteko chifukwa cha Yesu yekha ai, komanso kuti akaone Lazaro uja amene Iye adamuukitsa kwa akufa. Motero akulu a ansembe adaapangana zoti aphe ndi Lazaro yemwe, pakuti chifukwa cha iyeyo anthu ambiri ankaŵachokera nkumakhulupirira Yesu. M'maŵa mwake anthu ambirimbiri amene anali atabwera ku chikondwerero cha Paska chija, adamva kuti Yesu akubwera ku Yerusalemu. Motero adatenga nthambi za kanjedza natuluka kukamchingamira. Ankafuula kuti, “Ulemu kwa Mulungu! Ngwodala amene alikudza m'dzina la Ambuye! Idalitsidwe Mfumu ya Israele!” Tsono Yesu adapeza mwanawabulu nakwerapo, monga akunenera Malembo kuti, “Usaope, iwe mzinda wa Ziyoni. Ona, Mfumu yako ilikudza, yakwera pa mwanawabulu.” Pa nthaŵi imeneyo ophunzira ake sadazimvetse zimenezo. Koma Yesu atauka ndi ulemerero, iwo adakumbukira kuti zimenezi zidalembedwa kunena za Iye, ndipo kuti adamchitiradi zimenezi. Paja pamene Yesu adaaitana Lazaro kuti atuluke m'manda nkumuukitsa kwa akufa, panali anthu ambirimbiri. Tsono iwowo ankasimba m'mene adaaziwonera. Nchifukwa chake anthu onsewo adakamchingamira, popeza kuti anali atamva kuti Iye adaachita chizindikiro chozizwitsa chimenechi. Pamenepo Afarisi adayamba kuuzana kuti, “Mukuwonatu kuti sitikuphulapo kanthu konse. Onani anthu onse akumthamangira.” Koma panali Agriki ena pakati pa anthu amene adaakapembedza pa chikondwererocho. Iwowo adapita kwa Filipo, amene kwao kunali ku Betsaida wa ku Galileya, nakampempha kuti, “Pepani bambo, timati tidzaone Yesu.” Filipo adakauza Andrea, ndipo Andrea pamodzi ndi Filipoyo adakauza Yesu. Yesu adati, “Yafika nthaŵi yoti Mwana wa Munthu alandire ulemerero wake. Kunena zoona, mbeu ya tirigu imakhalabe imodzi yomweyo ngati siigwa m'nthaka nkufa. Koma ikafa, imabala zipatso zambiri. Munthu amene amakonda moyo wake, adzautaya, koma amene saikapo mtima pa moyo wake pansi pano, adzausungira ku moyo wosatha. Ngati munthu anditumikira Ine, anditsatire, motero kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga. Munthu akanditumikira Ine, Atate anga adzamlemekeza.” “Tsopano mtima wanga wavutika. Nanga ndinene chiyani? Kodi ndinene kuti, ‘Atate, mundipulumutse ku nthaŵi iyi?’ Iyai, kwenikweni ndidadzera nthaŵi imeneyi. Atate, onetsani ulemerero wa dzina lanu.” Pamenepo kudamveka mau ochokera kumwamba akuti, “Ndauwonetsa ulemererowo ndipo ndidzauwonetsanso.” Panali khamu la anthu pamenepo. Tsono pamene adamva mauwo, adati, “Kwagunda bingu.” Koma ena adati, “Mngelo walankhula naye.” Yesu adaŵauza kuti, “Mauŵa amveka osati chifukwa cha Ine ai, koma chifukwa cha inu. Tsopano ndiyo nthaŵi yoti anthu a dziko lino lapansi aweruzidwe. Tsopano Satana, mfumu ya anthu ochimwa a dziko lino lapansi, adzaponyedwa kunja. Ndipo Ine, akadzandipachika, ndidzakokera anthu onse kwa Ine.” (Adaanena mau ameneŵa kuti aŵadziŵitse za m'mene analikudzafera.) Anthu aja adamuuza kuti, “Ife tidaŵerenga m'Malamulo mwathu kuti Mpulumutsi wolonjezedwa uja adzakhala ndi moyo mpaka muyaya. Nanga Inu mukuneneranji kuti Mwana wa Munthu ayenera kupachikidwa? Mwana wa Munthuyo ndani?” Apo Yesu adaŵauza kuti, “Kuŵala kukhalabe pakati panu, koma kanthaŵi pang'ono chabe. Yendani pamene kuŵalako kuli pakati panu, kuti mdima ungakugwereni. Munthu woyenda mu mdima saona kumene akupita. Nthaŵi ino pamene kuŵala kuli pakati panu, mukhulupirire kuŵalako, kuti mukhale anthu oyenda m'kuŵala.” Yesu atanena zimenezi, adachokapo nakabisala. Ngakhale Yesu adaachita zozizwitsa zambiri chotere pamaso pao, komabe iwo sadamkhulupirire. Zidaatero kuti zipherezere zimene mneneri Yesaya adaaneneratu kuti, “Ambuye, ndani wakhulupirira kulalika kwathu? Ndani wazindikira mphamvu za Ambuye pa zimenezi?” Iwo sadathe kukhulupirira, chifukwa paja Yesaya yemweyo adaanenanso kuti, “Mulungu adadetsa maso ao, ndipo adabunthitsa nzeru zao, kuti maso ao asaone, nzeru zao zisamvetse, kuti angatembenuke mtima, ndipo Ine ndingaŵachiritse.” Yesaya ponena mau amenewo, ankanena za Yesu, chifukwa adaaona ulemerero wake. Komabe ambiri mwa atsogoleri ao omwe adakhulupirira Yesu. Koma chifukwa cha Afarisi iwo sankanena zimenezo poyera. Ankaopa kuti angaŵadule ku mpingo. Ankakonda kuti azilandira ulemu kwa anthu koposa kulandira ulemu kwa Mulungu. Yesu adanena mokweza mau kuti, “Munthu wondikhulupirira, sakhulupirira Ine ndekha ai, koma amakhulupiriranso Iye amene adandituma. Ndipo munthu woona Ine, amaonanso Iye amene adandituma. Ine ndine kuŵala, ndipo ndidadza pansi pano, kuti munthu aliyense wokhulupirira Ine, asamayende mu mdima. Munthu akamva mau anga koma osaŵagwiritsa ntchito, Ine sindimzenga mlandu ai. Pakuti sindidadzere kudzazenga anthu mlandu, koma kudzaŵapulumutsa. Munthu amene akana Ine, ndipo salandira mau anga, alipo amene adzamuweruze. Adzazengedwa mlandu pa tsiku lomaliza chifukwa cha mau omwe ndakhala ndikulankhulaŵa. Pajatu sindidalankhule zochokera mwa Ine ndekha, koma Atate amene adandituma ndiwo adandilamula zoti ndinene, ndi momwe ndilankhulire. Ndipo ndikudziŵa kuti zimene amandilamula nzolinga ku moyo wosatha. Nchifukwa chake zimene ndimalankhula, ndimalankhula monga momwe Atate amandiwuzira.” Chikondwerero cha Paska chili pafupi, Yesu adaadziŵiratu kuti nthaŵi yake yafika yakuti achoke pansi pano kupita kwa Atate. Iye ankaŵakonda amene anali ake pansi pano, ndipo adaaŵakonda kotheratu. Tsono Yesu ndi ophunzira ake ankadya chakudya chamadzulo. Satana nkuti ataika kale mumtima mwa Yudasi, mwana wa Simoni Iskariote, maganizo akuti akapereke Yesu kwa adani ake. Yesu ankadziŵa kuti Atate adapereka zinthu zonse m'manja mwake. Ankadziŵanso kuti adachokera kwa Mulungu, ndipo kuti akubwerera kwa Mulungu. Choncho pamene analikudya, Yesu adaimirira, adavula mwinjiro wake, natenga nsalu yopukutira nkuimanga m'chiwuno. Atatero adathira madzi m'beseni, nayamba kutsuka mapazi a ophunzira ake, nkumaŵapukuta ndi nsalu yopukutira ija imene adaaimanga m'chiwuno. Pamene adafika pa Simoni Petro, iyeyo adati, “Ambuye, Inuyo nkundisambitsa ine mapazi?” Yesu adamuyankha kuti, “Zimene ndikuchitazi, sukuzidziŵa tsopano, koma udzazidziŵa m'tsogolo muno.” Petro adati, “Simudzandisambitsa konse mapazi.” Yesu adamuyankha kuti, “Ngati sindikusambitsa, ndiye kuti chako palibe.” Simoni Petro adati, “Ambuye, ngati ndi choncho, mutsuke osati mapazi anga okha, komanso manja anga ndi mutu womwe.” Yesu adamuuza kuti, “Munthu amene wasamba, wayera yense. Palibe chifukwa choti asambenso, koma kungosamba mapazi okha basi. Tsono inu mwayera, koma osati nonsenu ai.” Yesu ankamudziŵa munthu wodzampereka kwa adani ake, nchifukwa chake adaati, “Si nonsenu muli oyera.” Yesu atatsuka mapazi a ophunzira ake, adavalanso mwinjiro wake nakakhalanso podyera paja. Kenaka adaŵafunsa kuti, “Kodi mwazimvetsa zimene ndakuchitiranizi? Paja inu mumanditchula kuti, ‘Aphunzitsi’ ndiponso, ‘Ambuye.’ Apo mumalondola, pakuti ndine amene. Tsono ngati Ine Mbuye wanu ndi Mphunzitsi wanu ndakusambitsani mapazi anu, ndiye kuti inunso muyenera kumasambitsana mapazi. Ndakupatsani chitsanzo, kuti inunso muzichita monga momwe Ine ndakuchitirani inu. Kunena zoona, wantchito saposa mbuye wake, nthumwinso siiposa woituma. Ngati mudziŵa zimenezi, ndinu odala mukamazichita. “Mauŵa sindikunenera nonsenu ai. Ndikuŵadziŵa amene ndaŵasankha. Koma ziyenera kuchitikadi zimene Malembo adanena kuti, ‘Amene ankadya nane pamodzi, yemweyo ndiye adandiwukira.’ Ndikukuuziranitu zimenezi tsopano zisanachitike, kuti zikadzachitika, mudzakhulupirire kuti Ine ndinedi Ndilipo. Ndithu ndikunenetsa kuti wolandira aliyense amene ndamtuma, amalandira Ine. Ndipo wondilandira Ine, amalandira Iye amene adandituma.” Yesu atanena zimenezi, adayamba kuvutika mu mtima ndipo adati, “Ndinene poyera pano: mmodzi mwa inu andipereka kwa adani anga.” Ophunzira aja adayamba kupenyetsetsana, osadziŵa konse kuti akunena yani. Wophunzira wina, yemwe Yesu ankamukonda kwambiri, adaakhala pambali pa Yesu. Tsono Simoni Petro adamkodola nati, “Taŵafunsa, kodi akunena yani?” Pamenepo iyeyo adatsamira pachifukwa pa Yesu, namufunsa kuti, “Ambuye, mukunena yani kodi?” Yesu adati, “Yemwe ndimusunsire nkumupatsa mkate umene ndimunyemere ndi ameneyo.” Tsono atasunsa mkate wonyemawo adaupatsa Yudasi, mwana wa Simoni Iskariote. Yudasi atangolandira mkatewo, Satana adaloŵa mwa iye. Yesu adamuuza kuti, “Zimene ufuna kuchita, kachite mwamsanga.” Koma mwa amene ankadyawo panalibe ndi mmodzi yemwe amene adaamvetsa zimene adaamuuzazo. Popeza kuti Yudasi ankasunga thumba la ndalama, anzake ankayesa kuti Yesu akumuuza kuti, “Kagule zofunika paphwando pano,” kapena kuti akapereke kanthu kwa osauka. Yudasi atalandira mkate uja, pompo adatuluka. Nthaŵiyo nkuti kutada kale. Yudasi atatuluka, Yesu adati, “Tsopano Mwana wa Munthu walemekezedwa, ndipo mwa Iyeyu Mulungu walemekezedwa. Ngati Mulungu walemekezedwa mwa Iyeyu, Mulungu Mwini nayenso adzamlemekeza Iye, ndipo achita zimenezi tsopano apa. Ana anga, ndili nanube kanthaŵi pang'ono. Mudzandifunafuna, koma ndikukuuzani tsopano, monga ndidauziranso akulu a Ayuda kuti, ‘Kumene ndikupita Ine, inu simungathe kufikako.’ Ndikukupatsani lamulo latsopano, lakuti muzikondana. Monga momwe Ine ndidakukonderani, inunso muzikondana. Mukamakondana, anthu onse adzadziŵa kuti ndinudi ophunzira anga.” Simoni Petro adafunsa Yesu kuti, “Ambuye, mukupita kuti?” Yesu adati, “Kumene ndikupita, sungathe kunditsatira tsopano ai, koma udzanditsatira bwino lino.” Petro adamufunsa kuti, “Ambuye, chifukwa chiyani sindingathe kukutsatirani tsopano? Inetu nditha kutaya ngakhale moyo wanga chifukwa cha Inu.” Apo Yesu adati, “Iweyo kutaya moyo wako chifukwa cha Ine! Ndithu ndikunenetsa kuti tambala asanalire, ukhala utandikana katatu kuti Ine sundidziŵa.” Yesu adauza ophunzira akewo kuti “Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu, khulupirirani Inenso. M'nyumba mwa Atate anga muli malo ambiri okhalamo. Kukadakhala kuti mulibe malo, ndikadakuuzani. Ndikupita kukakukonzerani malo. Ndipo ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengani, kuti inunso mukakhale kumene kuli Ine. Ndipo kumene ndikupita Ineko, njira yake mukuidziŵa.” Tomasi adati, “Ambuye, sitikudziŵa kumene mukupita, nanga njira yake tingaidziŵe bwanji?” Yesu adamuyankha kuti, “Ineyo ndine njira, ndine choona ndiponso moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate ngati sadzera mwa Ine. Mukadandidziŵa Ine, Atate anganso mukadaŵadziŵa. Kuyambira tsopano mukuŵadziŵa ndipo mwaŵaona.” Filipo adati, “Ambuye, tiwonetseni Atatewo, mukatero tikhutira.” Yesu adamuyankha kuti, “Iwe Filipo, ndakhala nanu nthaŵi yonseyi, ndipo sunandidziŵebe? Amene waona Ine, waonanso Atate. Nanga bwanji ukuti, ‘Tiwonetseni Atate?’ Kodi sukukhulupirira kuti Ine ndimakhala mwa Atate, ndipo Atate amakhala mwa Ine? Mau amene ndimakuuzani sachokera kwa Ine ndekha ai, koma Atate amene amakhala mwa Ine, ndiwo amagwira ntchito yao. Mundikhulupirire kuti Ine ndimakhala mwa Atate ndipo Atate amakhala mwa Ine. Kupanda apo, khulupiriranitu chifukwa cha ntchito zanga zomwezo. Ndithu ndikunenetsa kuti amene amandikhulupirira, ntchito zomwe ndimachita Ine, nayenso adzazichita. Ndipo adzachita zoposa pamenepa, chifukwa ndikupita kwa Atate. Chilichonse chomwe mudzachipemphe potchula dzina langa ndidzachita, kuti Atate adzalemekezedwe mwa Mwana. Ngati mudzandipempha kanthu potchula dzina langa ndidzakachitadi.” “Ngati mundikonda, muzidzatsata malamulo anga. Pamenepo ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthaŵi zonse. Nkhosweyo ndi Mzimu wodziŵitsa zoona. Anthu ongokonda zapansipano sangathe kumlandira ai, chifukwa samuwona kapena kumdziŵa. Koma inu mumamdziŵa, chifukwa amakhala ndi inu, ndipo adzakhala mwa inu. Sindidzakusiyani nokha kuti mukhale ana amasiye. Ndidzabweranso kwa inu. Kwangotsala kanthaŵi pang'ono, ndipo anthu ongokonda zapansipano sadzandiwonanso, koma inu mudzandiwona. Popeza kuti Ine ndili ndi moyo, inunso mudzakhala ndi moyo. Tsiku limenelo mudzadziŵa kuti Ine ndimakhala mwa Atate, ndipo inu mumakhala mwa Ine, monga Ine ndimakhala mwa inu. “Munthu amene alandira malamulo anga naŵatsata, ndiye amandikonda. Ndipo amene andikonda Ine, Atate anga adzamkonda. Inenso ndidzamkonda munthuyo, ndipo ndidzadziwonetsa kwa iye.” Yudasi, osati Iskariote uja ai, adamufunsa kuti, “Ambuye zatani kuti muziti mudzadziwonetsa kwa ife, koma osati kwa anthu onse?” Yesu adati, “Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine. Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye. Munthu amene sandikonda, satsata zimene ndanena Ine. Mau amene mulikumvaŵa si angatu ai, koma ndi a Atate amene adandituma. “Zimenezi ndakuuzani ndikadali nanu. Koma Nkhoswe ija, Mzimu Woyera amene Atate adzamtuma m'dzina langa, ndiye adzakuphunzitseni zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndidakuuzani. “Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa. Mwandimva ndikukuuzani kuti, ‘Ndikupita, koma ndidzabweranso kwa inu.’ Mukadandikonda, bwenzi mutakondwera kuti ndikupita kwa Atate, chifukwa Atate ngoposa Ine. Ndakuuziranitu zimenezi tsopano zisanachitike, kuti zikadzachitika, mudzakhulupirire. Sindilankhula nanunso zambiri tsopano ai, pakuti Satana, mfumu ya anthu ochimwa a dziko lapansi, alikudza. Iyeyo alibe mphamvu pa Ine, koma anthu onse ayenera kudziŵa kuti ndimakonda Atate, nchifukwa chake ndikuchita monga Atate adandilamulira. Tiyeni, tizipita.” “Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate anga ndi mlimi. Iwo amadula nthambi iliyonse mwa Ine imene siibala zipatso. Ndipo nthambi iliyonse yobala zipatso, amaitengulira kuti ibale zipatso zambiri koposa kale. Inu mwayera kale chifukwa cha mau amene ndakuuzani. Khalani mwa Ine, ndipo Inenso ndidzakhala mwa inu. Nthambi siingathe kubala zipatso payokha ngati siikhala pa mtengo wake. Momwemonso inu ngati simukhala mwa Ine. “Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi. Munthu wokhala mwa Ine, ndi Inenso mwa iye, amabereka zipatso zambiri. Pajatu popanda Ine simungathe kuchita kanthu. Ngati munthu sakhala mwa Ine, amamtaya kunja monga nthambi yodulidwa, ndipo amauma. Nthambi zotere amazitola, naziponya pa moto ndipo zimapsa. Ngati mukhala mwa Ine, ndipo mau anga akhala mwa inu, mupemphe chilichonse chimene mungachifune, ndipo mudzachilandiradi. Atate anga amalemekezedwa pamene mubereka zipatso zambiri, ndipo pakutero mumaonetsa kuti ndinu ophunzira anga enieni. “Monga momwe Atate andikondera, Inenso ndakukondani. Muzikhala m'chikondi changachi. Ngati mutsata malamulo anga, mudzakhala m'chikondi changa, monga momwe Ine ndatsatira malamulo a Atate anga, ndipo ndimakhala m'chikondi chao. “Ndakuuzani zimenezi kuti chimwemwe changa chikhale mwa inu, kuti chimwemwe chanu chikhale chathunthu. Lamulo langa ndi lakuti muzikondana monga momwe Ine ndakukonderani. Palibe munthu amene ali ndi chikondi choposa ichi chakuti nkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake. Inu ndinu abwenzi anga ngati muchita zimene ndikulamulani. Sindikutchulaninso antchito ai, pakuti wantchito sadziŵa zimene mbuye wake akuchita. Koma ndikukutchulani abwenzi, chifukwa zonse zimene ndidamva kwa Atate anga, ndidakudziŵitsani. Si ndinutu mudandisankha Ine ai, koma ndine ndidakusankhani inu. Ndipo ndidakupatulani kuti mukabereke zipatso, zipatso zake zokhalitsa. Motero chilichonse chimene mungapemphe Atate potchula dzina langa, adzakupatsani. Choncho lamulo langa ndi lakuti muzikondana.” “Ngati anthu odalira zapansipano adana nanu, kumbukirani kuti adadana ndi Ine asanadane nanu. Mukadakhala a mkhalidwe wao, akadakukondani chifukwa cha kukhala anzao. Koma amadana nanu, chifukwa Ine ndidakusankhani pakati pa iwo, motero sindinu anzao. Kumbukirani mau aja amene ndidakuuzani kuti, ‘Wantchito saposa mbuye wake.’ Ngati Ine adandisautsa, inunso adzakusautsani. Ngati adamvera mau anga, adzamvera mau anunso. Koma adzakuchitirani zonsezi chifukwa cha Ine, popeza kuti samdziŵa amene adandituma. Ndikadapanda kubwera ndi kulankhula nawo, sakadakhala ndi mlandu. Koma tsopano alibe choti nkukanira mlandu wao. Munthu wodana ndi Ine, amadana ndi Atate anganso. Ndikadapanda kuchita pakati pao zimene wina aliyense sadazichite, sibwenzi atakhala ndi mlandu. Koma tsopano adaziwonadi, komabe akudana nane ndiponso ndi Atate anga. Koma zatere kuti zipherezere zimene zidalembedwa m'buku lao la Malamulo kuti, ‘Adadana nane popanda chifukwa.’ “Koma pali Nkhoswe imene ndidzakutumizireni kuchokera kwa Atate. Nkhosweyo ndi Mzimu wa choona wofumira mwa Atate. Iyeyo akadzabwera, adzandichitira umboni. Inunso mudzandichitira umboni, popeza kuti mwakhala nane kuyambira pa chiyambi.” “Ndakuuziranitu zonsezi kuti mungadzataye mtima. Adzakudulani ku mpingo. Komanso nthaŵi ilikudza yakuti aliyense amene adzakuphani, adzayesa kuti akutumikira Mulungu. Adzachita zimenezi chifukwa sadadziŵe Atate kapenanso Ine. Koma ndimati muzimve zimenezi kuti nthaŵi yakeyo ikadzafika, mudzakumbukire kuti ndidaakuuziranitu.” “Sindidakuuzeni zimenezi poyamba paja ai, chifukwa ndinali nanu pamodzi. Koma tsopano ndikupita kwa amene adandituma, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe mwa inu wondifunsa kuti, ‘Mukupita kuti?’ M'mitima mwanu mwadzaza chisoni chifukwa ndakuuzani zimenezi. Komabe ndikukuuzani zoona, kuti nkwabwino koposa kwa inu kuti ndichoke. Pakuti ngati sindichoka, Nkhoswe ija siidzabwera kwa inu. Koma ngati ndipita, ndidzaitumiza kwa inu. Ndipo Iyeyu atafika, adzaŵatsimikiza anthu a pansi pano kuti ngolakwa pa za kuchimwa, za kulungama, ndiponso za kuweruza. Ngolakwa pa za kuchimwa, chifukwa sandikhulupirira. Ngolakwa pa za kulungama, chifukwa ndikupita kwa Atate ndipo simudzandiwonanso. Ngolakwa pa za kuweruza, chifukwa Satana, mfumu ya anthu oipa a dziko lino lapansi, waweruzidwa kale. “Ndili nawo mau ena ambiri oti ndikuuzeni, koma simungathe kuŵamvetsa tsopano ai. Koma akadzafika Mzimu wodziŵitsa zoona uja adzakuphunzitsani zoona zonse. Pakuti sadzalankhula zochokera kwa Iye yekha ai, koma zilizonse zimene Atate adzamuuze, ndizo zimene adzalankhula. Ndipo adzakudziŵitsani zinthu zam'tsogolo. Adzandilemekeza, pakuti adzatenga zochokera kwa Ine nadzakudziŵitsani. Zonse za Atate nzanga. Nchifukwa chake ndanena kuti adzatenga zochokera kwa Ine, nadzakudziŵitsani inu.” “Kanthaŵi pang'ono ndipo simudzandiwonanso, koma patapitanso kanthaŵi pang'ono, mudzandiwona.” Ophunzira ake ena adayamba kufunsana kuti, “Kodi nchiyani akutiwuzachi? Akuti, ‘Kanthaŵi pang'ono ndipo simudzandiwonanso, koma patapitanso kanthaŵi pang'ono, mudzandiwona.’ Akutinso, ‘Chifukwa ndikupita kwa Atate.’ Kodi nchiyani akunenachi kuti, ‘Kanthaŵi pang'ono?’ Sitikumvetsa zimene akufuna kunena.” Yesu adaazindikira kuti ophunzirawo akufuna kumufunsa. Choncho adati, “Kodi mukufunsana za mau amene ndanenaŵa akuti, ‘Kanthaŵi pang'ono ndipo simudzandiwonanso, koma patapitanso kanthaŵi pang'ono, mudzandiwona?’ Ndithu ndikunenetsa kuti inu mudzalira ndi kukhuza, koma anthu odalira zapansi pano adzakondwa. Inu mudzamva chisoni, koma chisoni chanu chidzasanduka chimwemwe. Pa nthaŵi yochira mai amavutika chifukwa nthaŵi yake yafika. Koma pamene wabadwa mwana, saganizakonso za kuzunzikako, chifukwa cha chimwemwe chakuti kunja kuno kwabadwa mwana. Chomwecho inunso mukuvutika tsopano, koma ndidzakuwonaninso. Pamenepo mtima wanu udzakondwa, ndipo palibe munthu amene adzakulandani chimwemwe chanucho. Pa tsiku limenelo simudzandifunsa kanthu. Ndithu ndikunenetsa kuti chilichonse chimene mungapemphe kwa Atate potchula dzina langa, adzakupatsani. Mpaka tsopano simunapemphe kanthu potchula dzina langa. Pemphani ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chikhale chathunthu.” “Ndakuuzani zimenezi mophiphiritsa. Nthaŵi ilikudza pamene sindidzalankhula nanunso mophiphiritsa, koma ndidzakudziŵitsani momveka za Atate. Tsiku limenelo mudzapempha potchula dzina langa, ndipo sindikuti Ine ndidzakupempherani kwa Atate ai, pakuti okukondani ndi Atate amene. Amakukondani chifukwa mumandikonda, ndipo mumakhulupirira kuti ndidachokera kwa Iwo. Ndidachokeradi kwa Atate kudza pansi pano. Tsopano ndikuchokanso pansi pano kupita kwa Atate.” Ophunzira ake adati, “Apo ndipo. Tsopano mukulankhula momveka, osatinso mophiphiritsa ai. Tsopano tadziŵa kuti mumadziŵa zonse, ndipo palibenso chifukwa choti munthu akufunseni mafunso. Nchifukwa chake tikukhulupirira kuti ndinu ochokera kwa Mulungu.” Yesu adaŵayankha kuti, “Kani mwakhulupiriratu tsopano? Nthaŵi ilikudza, ndipo yafika kale, pamene mudzabalalikana aliyense kunka kwao, Ine kundisiya ndekha. Komabe sindili ndekha, pakuti Atate ali nane. Ndakuuzani zimenezi kuti mukhale nawo mtendere pakukhulupirira Ine. M'dziko lapansi mudzaona masautso, koma limbikani, Ine ndagonjetsa mphamvu zoipa za dziko lapansi.” Yesu atanena zimenezi, adayang'ana kumwamba nati, “Atate, yafika nthaŵi. Lemekezani Mwana wanu, kuti Mwanayo akulemekezeni Inu. Pajatu mudampatsa mphamvu zolamulira anthu onse, kuti apereke moyo wosatha kwa onse amene mudampatsa. Moyo wosathawo ndi wakuti akudziŵeni Inu, amene nokhanu ndinu Mulungu weniweni, ndipo adziŵenso Yesu Khristu amene mudamtuma. Ndakulemekezani pansi pano pakutsiriza ntchito imene mudandipatsa. Ndipo tsopano Inu Atate mundilemekeze pamaso panu ndi ulemerero uja umene ndinali nawo kwa Inu lisanalengedwe dziko lapansi.” “Amene mudaŵapatula mwa anthu onse ndi kundipatsa Ine, ndaŵadziŵitsa dzina lanu. Anali anu, Inu mudaŵapereka kwa Ine, ndipo adasunga mau anu. Tsopano akudziŵa kuti zonse zimene mudandipatsa nzochokera kwa Inu. Pakuti ndaŵapatsa mau amene mudandiwuza Ine, ndipo aŵalandira. Akudziŵadi kuti ndidachokera kwa Inu, ndipo sakayika kuti ndinu mudandituma. “Ine ndikuŵapempherera. Sindikupempherera anthu ena onse, koma ndikupempherera iwoŵa amene mudandipatsa, chifukwa ndi anu. Zanga zonse nzanu, monga zanu zonse nzanga, motero ndimalemekezedwa mwa iwowo. Ndilikudza kwa Inu. Ine sindikhalanso pansi pano ai, koma iwoŵa akhala pansi pano. Atate oyera, asungeni iwoŵa m'dzina lanu limene mudandipatsa, kuti akhale amodzi monga ife. Pamene ndinali nawo pamodzi, ndinkaŵasunga ndi mphamvu za dzina lanu, zimene mudandipatsa. Ndidaŵalondoloza bwino, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adatayika, kupatula yekha uja amene adayenera kutayika, kuti zipherezere zimene Malembo adaaneneratu. “Tsopano ndilikudza kwa Inu. Ndikulankhula zimenezi pamene ndili pansi pano, kuti chimwemwe changa chikhalenso chodzaza mwa iwowo. Ndaŵaphunzitsa mau anu. Anthu odalira zapansipano amadana nawo, chifukwa iwo sali anzao, monga Inenso sindili mnzao. Sindikupempha kuti muŵachotse pansi pano ai, koma kuti muŵatchinjirize kwa Woipa uja. Iwo sali a dziko lapansi, monga Inenso sindili wa dziko lapansi. Muziŵapatula ndi mau anu kuti akhale anthu anu. Mau anuwo ngoona zedi. Monga mudandituma Ine pansi pano, Inenso ndaŵatuma pansi pano. Ndipo chifukwa cha iwoŵa ndikudzipereka kwa Inu, kuti iwonso akhale odzipereka moonadi kwa Inu.” “Sindikupempherera iwo okhaŵa ai, komanso amene adzandikhulupirira chifukwa cha mau ao. Ndikuŵapempherera kuti iwo onse akhale amodzi. Monga Inu Atate mumakhala mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, iwonso akhale mwa Ife. Motero anthu onse adzakhulupirira kuti mudandituma. Ulemerero womwewo umene mudandipatsa, ndaŵapatsanso iwoŵa. Akhale amodzi monga Ife tili amodzi. Ine ndikhale mwa iwo, Inu mwa Ine, kuti akhale amodzi kwenikweni. Motero anthu onse adzazindikira kuti mudandituma ndinu, ndipo kuti mumaŵakonda monga momwe mumandikondera Ine. “Atate, ndifuna kuti amene mudandipatsa, iwonso akhale pamodzi ndi Ine kumene ndili. Ndifuna kuti aone ulemerero wanga umene mudandipatsa, chifukwa mudandikonda dziko lapansi lisanalengedwe. Atate olungama, anthu odalira zapansipano sadakudziŵeni ai, koma Ine ndimakudziŵani, ndipo aŵa ali panoŵa akudziŵa kuti ndinu mudandituma. Ndidaŵadziŵitsa dzina lanu, ndipo ndidzaŵaphunzitsabe. Ndifuna kuti chikondi chimene mumandikonda nacho, chikhalenso mwa iwo, ndipo Ine mwa iwo.” Yesu atanena zimenezi, adapita ndi ophunzira ake kutsidya kwa kamtsinje ka Kedroni. Kumeneko kunali munda, ndipo adaloŵa m'menemo. Yudasi yemwe, amene adapereka Yesu kwa adani ake, ankaŵadziŵa malowo, pakuti Yesu ankapita kumeneko kaŵirikaŵiri ndi ophunzira ake. Yudasiyo adatenga gulu la asilikali achiroma pamodzi ndi asilikali a ku Nyumba ya Mulungu amene akulu a ansembe ndi Afarisi adaaŵatuma. Iwo adapita kumundako atatenga nyale ndi miyuni ndi zida zankhondo. Yesu adaadziŵiratu zonse zimene zinalikudzamugwera. Nchifukwa chake Iye adaima poyera, naŵafunsa kuti, “Kodi mukufuna yani?” Adamuyankha kuti, “Tikufuna Yesu wa ku Nazarete.” Yesu adati, “Ndine, ndilipo.” Yudasi, wompereka kwa adani ake uja, anali nao pomwepo. Pamene Yesu adaŵayankha kuti, “Ndine, ndilipo,” iwo adabwerera m'mbuyo nagwa pansi. Yesu adaŵafunsanso kuti, “Mukufuna yani kodi?” Iwo aja adati “Tikufuna Yesu wa ku Nazarete.” Yesu adati, “Ndakuuzani kuti ndine, ndilipo. Tsono ngati mukufuna Ine, aŵa alekeni apite.” (Adaatero kuti zipherezere zimene Iye adaanena kale kuti, “Sindidatayepo ndi mmodzi yemwe mwa amene mudandipatsa.”) Simoni Petro anali ndi lupanga. Adalisolola, natema kapolo wa mkulu wa ansembe onse, mpaka kumusenga khutu la ku dzanja lamanja. Kapoloyo dzina lake anali Malkusi. Apo Yesu adauza Petro kuti, “Bwezera lupanga lako m'chimake. Kodi ukuti ndisamwe chikho cha masautso chimene Atate andipatsa?” Gulu la asilikali achiroma lija, pamodzi ndi mtsogoleri wao, ndiponso asilikali achiyuda, adagwira Yesu nammanga. Poyamba adapita naye kwa Anasi, chifukwa anali mpongozi wa Kayafa, amene anali mkulu wa ansembe onse chaka chimenecho. Kayafayo ndi yemwe uja amene adaalangiza anzake kuti nkwabwino koposa kuti munthu mmodzi afe m'malo mwa anthu onse. Simoni Petro ndi wophunzira wina adatsatira Yesu. Wophunzira winayo anali wodziŵika kwa mkulu wa ansembe onse. Tsono iye adaloŵa pamodzi ndi Yesu m'bwalo la nyumba ya mkulu wa ansembeyo. Koma Petro adaima pa khomo kunja. Wophunzira wina uja, amene anali wodziŵikayo, adatuluka nakalankhula ndi mtsikana wolonda pa khomo, nkumuloŵetsa Petroyo. Mtsikanayo adafunsa Petro kuti, “Kodi inu sindinunso mmodzi mwa ophunzira a munthuyu?” Iye adati, “Ineyo? Iyai.” Antchito pamodzi ndi asilikali achiyuda aja adaaimirira pamenepo atasonkha moto nkumaotha, chifukwa kunkazizira. Petro nayenso adaaimirira pomwepo nkumaotha nao motowo. Tsono mkulu wa ansembe onse adafunsa Yesu za ophunzira ake, ndiponso za zimene Iye ankaphunzitsa. Yesu adati, “Ine ndinkalankhula mosabisa pamaso pa anthu onse. Ndinkaphunzitsa m'nyumba zamapemphero ndiponso m'Nyumba ya Mulungu, m'mene anthu onse amasonkhana. Sindidalankhule kanthu mobisa ai. Nanga tsono mukundifunsiranji Ineyo? Funsani amene adamva zomwe ndinkaŵauza. Iwowo akudziŵa zimene ndinkanena.” Atanena zimenezi, mmodzi mwa asilikali oimirira pomwepo adamenya Yesu kumaso, adati, “Ungayankhe choncho kwa mkulu wa ansembe onse?” Yesu adamuyankha kuti, “Ngati ndalankhula moipa, chitchule choipacho. Koma ngati ndalankhula moona, ukundimenyeranji?” Anasi adatumiza Yesu ali chimangire kwa Kayafa, mkulu wa ansembe onse. Simoni Petro anali chililibe akuwotha nao moto. Tsono ena adamufunsa kuti, “Kodi iwenso sindiwe mmodzi mwa ophunzira a munthu uja?” Petro adakana, adati, “Iyai.” Wantchito wina wa mkulu wa ansembe onse, mbale wa munthu uja amene Petro adaamusenga khutu, adamufunsa kuti, “Kodi sindidakuwone m'munda muja uli naye?” Petro adakananso, nthaŵi yomweyo tambala adalira. Adamtenga Yesu kuchokera kwa Kayafa kupita naye ku bwalo la bwanamkubwa. Akuluakulu a Ayuda sadaloŵe nao m'bwalo la bwanamkubwalo, kuwopa kuti angaipitsidwe, pakuti ankafuna kudya phwando la Paska. Motero Pilato adatulukira kwa iwo naŵafunsa kuti, “Mwampeza cholakwa chanji munthuyu?” Iwo adati, “Akadapanda kuchita choipa ameneyu, sibwenzi titadzampereka kwa inu ai.” Choncho Pilato adaŵauza kuti, “Mtengenitu tsono inuyo, mukamuweruze potsata malamulo anu.” Koma Ayudawo adati, “Ife sitiloledwa kupha munthu ai.” (Zidaatero kuti zipherezere zimene Yesu adaanena za imfa yake.) Pilato adaloŵanso m'nyumba yake ija, naitana Yesu. Adamufunsa kuti, “Kodi iwe, ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Yesu adati, “Kodi mukunena zimenezi mwa inu nokha, kapena ena adakuuzani za Ine?” Pilato adati, “Ine ndine Myuda kodi? Anthu a mtundu wako womwe ndiponso akulu a ansembe ndiwo akupereka kwa ine. Udachita chiyani?” Yesu adayankha kuti, “Ufumu wanga si wapansipano ai. Ufumu wanga ukadakhala wapansipano, bwenzi anyamata anga atamenya nkhondo kuti ndisaperekedwe kwa akulu a Ayuda. Komatu ai, ufumu wanga si wapansipano.” Pilato adati, “Tsono ndiye kuti ndiwedi mfumu, ati?” Yesu adati, “Mwanena nokha kuti ndine mfumu. Ine ndidabwera pansi pano ndipo ndidabadwa kuti ndidzachitire umboni choona. Aliyense wokonda choona amamva mau anga.” Pilato adamufunsa kuti, “Choona nchiyaninso?” Pilato atanena mau ameneŵa, adatulukiranso kwa Ayuda, naŵauza kuti, “Ine munthuyu sindikumpeza chifukwa chilichonse. Koma potsata chizoloŵezi chanu, pa nthaŵi ya chikondwerero cha Paska ndimakumasulirani mkaidi mmodzi. Tsono kodi mukufuna kuti ndikumasulireni Mfumu ya Ayudayi?” Pamenepo iwo adafuulanso kuti, “Ameneyu ai, koma Barabasi.” (Barabasiyo anali chigaŵenga.) Pamenepo Pilato adalamula kuti atenge Yesu ndi kumkwapula. Tsono asilikali adaluka nsangamutu yaminga naiika pamutu pake. Adamuveka chovala chofiirira, nadza kwa Iye nkumanena kuti, “Tikuwoneni, mfumu ya Ayuda!” Ndipo adayamba kumuwomba makofi. Pilato adatulukanso nauza Ayudawo kuti, “Onani, ndikumtulutsira kuli inu kuno kuti mudziŵe kuti sindikumpeza chifukwa chilichonse.” Pamene Yesu adatuluka, atavala nsangamutu ija ndi chovala chofiirira chija, Pilato adati, “Nayutu munthu uja.” Akulu a ansembe ndi asilikali a ku Nyumba ya Mulungu aja ataona Yesu, adafuula kuti, “Mpachikeni! Mpachikeni!” Pilato adaŵauza kuti, “Mtengeni inuyo mukampachike, ine ndiye sindikumpeza chifukwa.” Anthuwo adati, “Ife tili ndi lamulo, ndipo potsata lamulolo ayenera kufa, chifukwa ankati, ‘Ndine Mwana wa Mulungu.’ ” Pamene Pilato adamva mau ameneŵa, adachita mantha kwabasi. Tsono adaloŵanso m'nyumba ya bwanamkubwa ija nafunsa Yesu kuti, “Kodi iwe, kwanu nkuti?” Koma Yesu sadayankhe kanthu. Pamenepo Pilato adamufunsa kuti, “Sukundiyankha? Kodi sukudziŵa kuti ine ndili ndi mphamvu zokumasula, ndiponso mphamvu zokupachika?” Yesu adati, “Akadapanda kukupatsani mphamvu zimenezo Mulungu, sibwenzi mutakhala nazo konse mphamvu pa Ine. Nchifukwa chake amene wandipereka kwa inu ali ndi tchimo lalikulu koposa.” Atamva mau ameneŵa, Pilato adafuna ndithu kummasula Yesu. Koma Ayuda adafuula kuti, “Mukammasula ameneyu, sindinu bwenzi la Mfumu ya ku Roma. Aliyense wodziyesa mfumu, ngwoukira Mfumu ya ku Romayo.” Pilato atamva zimenezo, adatulutsa Yesu, nakakhala pa mpando woweruzira milandu, pa malo otchedwa “Bwalo lamiyala” (pa Chiyuda amati “Gabata.”) Linali tsiku lokonzekera chikondwerero cha Paska, ndipo nkuti nthaŵi ili ngati 12 koloko masana. Pilato adauza Ayuda kuti, “Nayitu Mfumu yanu.” Koma iwo adafuula kuti, “Mchotseni! Mchotseni! Kampachikeni pa mtanda!” Pilato adaŵafunsa kuti, “Ndipachike Mfumu yanu kodi?” Akulu a ansembe adati, “Tilibe mfumu ina ai, koma Mfumu ya ku Roma yokha.” Pamenepo Pilato adapereka Yesu kwa iwo kuti akampachike pa mtanda. Asilikali aja adamtenga Yesu. Iye atasenza mtanda wake, adatuluka naye mu mzinda kupita ku malo otchedwa “Malo a Chibade cha Mutu” (pa Chiyuda amati “Gologota.”) Kumeneko adampachika pa mtanda. Adapachikanso anthu ena aŵiri, wina ku dzanja lake lamanja, wina ku dzanja lake lamanzere, Yesu pakati. Pilato adalemba chidziŵitso nachiika pamtandapo. Adaalembapo kuti, “Yesu wa ku Nazarete, Mfumu ya Ayuda.” Ayuda ambiri adachiŵerenga chidziŵitsocho, chifukwa pamalo pamene Yesu adaapachikidwapo panali pafupi ndi mzinda wa Yerusalemu. Chidziŵitsocho chidalembedwa m'chilankhulo cha Ayuda, cha Aroma, ndiponso cha Agriki. Akulu a ansembe a Ayuda adauza Pilato kuti, “Musalembe kuti, ‘Mfumu ya Ayuda’ ai, koma kuti, ‘Iyeyu ankati Ndine Mfumu ya Ayuda.’ ” Koma Pilato adati, “Zimene ndalemba, ndalemba ndatha basi.” Asilikali aja atapachika Yesu, adatenga zovala zake, nazigaŵa panai, msilikali aliyense chigawo chake. Adatenganso mkanjo wake. Mkanjowo unali wolukidwa kuyambira pamwamba mpaka pansi, opanda msoko. Tsono asilikaliwo adauzana kuti, “Tisaung'ambe, koma tichite mayere kuti tiwone ukhala wa yani.” Zidaayenda choncho kuti zipherezere zimene Malembo adanena kuti, “Adagaŵana zovala zanga, ndipo mkanjo wanga adauchitira mayere.” Zimenezi adachitadi asilikali aja. Pafupi ndi mtanda wa Yesu padaaimirira amai ake, ndi mbale wa amai akewo, Maria mkazi wa Kleopa, ndi Maria wa ku Magadala. Pamene Yesu adaona amai ake ndi wophunzira uja amene Iye ankamukonda kwambiri, akuimirira pafupi, adauza amai ake kuti, “Mai, nayu mwana wanu.” Adauzanso wophunzirayo kuti, “Naŵa amai ako.” Ndipo kuyambira pamenepo wophunzirayo adaŵatenga amaiwo kumakaŵasamala kwao. Yesu adaadziŵa kuti tsopano zonse wakwaniritsa. Tsono kuti zipherezere zimene Malembo adaanena, Iye adati, “Ndili ndi ludzu.” Pomwepo panali mbiya yodzaza ndi vinyo wosasa. Asilikali aja adaviika chinkhupule m'vinyo wosasayo, nkuchitsomeka ku kamtengo ka hisope, nachifikitsa pakamwa pake. Yesu atalandira vinyo wosasayo adati, “Zonse ndakwaniritsa.” Kenaka adaŵeramitsa mutu, napereka mzimu. Linali tsiku lokonzekera chikondwerero cha Paska. Akulu a Ayuda sadafune kuti mitemboyo ikhalebe pa mtanda pa tsiku la Sabata, chifukwa Lasabata limenelo linali lalikulu. Nchifukwa chake adakapempha Pilato kuti alamule kuti akathyole miyendo ya anthu opachikidwa aja, nkuŵachotsa. Tsono asilikali adabwera, nathyola miyendo ya mmodzi mwa aŵiri aja amene adaapachikidwa pamodzi ndi Yesu. Adateronso ndi mnzake uja. Koma pamene adafika pa Yesu, poona kuti wafa kale, sadathyole miyendo yake. Koma mmodzi mwa asilikali aja adamubaya m'nthiti mwake ndi mkondo, ndipo nthaŵi yomweyo mudatuluka magazi ndi madzi. Amene adaona zimenezi ndiye akuzichitira umboni, kuti inunso mukhulupirire. Umboni wakewo ngwoona, ndipo mwiniwakeyo akudziŵa kuti zimene akunena nzoona. Izi zidaatero kuti zipherezere zimene Malembo adanena kuti, “Sadzathyola fupa lake ndi limodzi lomwe.” Ndipo penanso Malembo akuti, “Anthu azidzamuyang'ana amene iwo adamubaya.” Pambuyo pake Yosefe wa ku Arimatea adapempha Pilato kuti amlole kukachotsa mtembo wa Yesu. (Yosefeyo anali wophunzira wa Yesu, koma mobisika, chifukwa choopa akulu a Ayuda.) Tsono Pilato atamlola, iye adakachotsa mtembowo. Kudabweranso Nikodemo, yemwe uja amene adaabwera kwa Yesu usiku poyamba paja. Iye adabwera ndi mafuta onunkhira a mure osanganiza ndi aloe, kulemera kwake ngati makilogaramu 32. Anthu aŵiriwo adatenga mtembo wa Yesu, naukulunga m'nsalu zoyera zabafuta pamodzi ndi zonunkhira zija, potsata mwambo wamaliro wachiyuda. Kumene Yesu adaapachikidwako kunali munda. Ndipo m'mundamo munali manda atsopano, amene anali asanaikemo munthu. Tsono popeza kuti linali tsiku la Ayuda lokonzekera chikondwerero cha Paska, ndipo mandawo anali pafupi, adaika Yesu m'menemo. Pa tsiku lotsatira Sabata ya Ayuda, m'mamaŵa ndithu kudakali kamdima, Maria wa ku Magadala adadza ku manda a Yesu. Adaona kuti chimwala chija chachotsedwa kale pa khomo la mandawo. Choncho adathamanga nakafika kwa Simoni Petro, ndi kwa wophunzira wina uja amene Yesu ankamukonda kwambiri. Adaŵauza kuti, “Aŵachotsa Ambuye m'manda muja, ndipo sitikudziŵa kumene akaŵaika.” Pamenepo Petro ndi wophunzira wina uja adatuluka napita ku manda. Onse aŵiri adathamanga pamodzi, koma wophunzira wina uja adathamanga kopambana Petro, nkuyambira ndiye kufika kumandako. Adaŵerama naona nsalu zija zili chikhalire, koma iye sadaloŵemo. Simoni Petro atafika akumutsatira, adaloŵa m'mandamo. Adaona nsalu zija zili chikhalire, ndiponso kansalu kamene kanali kumutu kwake. Kansaluko sikanali pamodzi ndi nsalu zina zija, koma padera pakokha, kali chipindire. Pamenepo wophunzira wina uja, amene adaayambira kufika ku manda, nayenso adaloŵa; ndipo ataona zimenezi, adakhulupirira. Mpaka nthaŵi imeneyo iwo aja anali asanamvetse Malembo akuti Yesu adzayenera kuuka kwa akufa. Pambuyo pake ophunzirawo adabwerera kwao. Maria adakhalabe chilili panja pafupi ndi manda, akulira. Akulira choncho, adaŵerama kusuzumira m'mandamo, naona angelo aŵiri ovala zovala zoyera. Angelowo adaakhala pansi, wina kumutu, wina kumapazi pamalo pamene padaagona mtembo wa Yesu paja. Iwo adamufunsa kuti, “Inu mai, mukuliranji?” Iye adati, “Chifukwa aŵachotsa Ambuye anga ndipo sindikudziŵa kumene akaŵaika.” Atanena zimenezi adacheuka, naona Yesu ataimirira pomwepo, koma sadamzindikire kuti ndi Yesu. Tsono Yesu adamufunsa kuti, “Mai iwe, ukuliranji? Ukufuna yani?” Maria ankayesa kuti ndi wakumundako, motero adamuuza kuti, “Bambo, ngati mwaŵachotsa ndinu, mundiwuze kumene mwakaŵaika, kuti ndikaŵatenge.” Yesu adati, “Maria!” Iye adacheuka, nanena kuti, “Raboni!” (Ndiye kuti “Aphunzitsi” pa chihebri) Yesu adamuuza kuti, “Usandigwire, pakuti sindinakwerebe kupita kwa Atate. Koma pita kwa abale anga, ukaŵauze kuti, ‘Ndikukwera kupita kwa Atate anga, omwe ali Atate anunso, Mulungu wanga, yemwe ali Mulungu wanunso.’ ” Maria wa ku Magadalayo adapita, nakauza ophunzira aja kuti, “Ndaŵaona Ambuye,” ndipo adaŵakambira zimene Ambuyewo adaamtuma. Madzulo kutada pa tsiku Lamulungu lomwelo, ophunzira aja anali pamodzi. Zitseko zinali zokhoma, chifukwa ankaopa akulu a Ayuda. Tsono Yesu adadza naimirira pakati pao nkunena kuti, “Mtendere ukhale nanu!” Atatero, adaŵaonetsa manja ake ndi m'nthiti mwake, ndipo ophunzira aja adakondwa kwambiri poŵaona Ambuyewo. Yesu adatinso, “Mtendere ukhale nanu. Monga Atate adandituma, Inenso ndikukutumani.” Pambuyo pake adaŵauzira mpweya nati, “Landirani Mzimu Woyera. Anthu amene mudzaŵakhululukira machimo ao, adzakhululukidwadi, koma amene simudzaŵakhululukira, sadzakhululukidwa ai.” Mmodzi mwa ophunzira aja khumi ndi aŵiri, Tomasi (wotchedwa Didimo), sanali pamodzi ndi anzake pamene Yesu adaabwera. Tsono ophunzira anzake aja adamuuza kuti, “Ife taŵaonatu Ambuye.” Koma Tomasi adati, “Ndikapanda kuwona mabala a misomali m'manja mwao, ndi kupisa chala changa m'mabala a misomaliwo, ndipo ndikapanda kupisa dzanja langa m'nthiti mwao, sindingakhulupirire konse.” Patapita masiku asanu ndi atatu, ophunzira aja analinso m'nyumbamo, ndipo Tomasi anali nawo. Zitseko zinali chikhomere, koma Yesu adadza, naimirira pakati pao nati, “Mtendere ukhale nanu!” Atatero, adauza Tomasi kuti, “Ika chala chako apa, ona manja anga. Tambalitsa dzanja lako, ulipise m'nthiti mwangamu. Leka kukayika, uyambepo kukhulupirira.” Tomasi adati, “Ambuye anga! Mulungu wanga!” Yesu adati, “Kodi wakhulupirira chifukwa wandiwona? Ngwodala amene amakhulupirira ngakhale sadaone.” Yesu adachitanso zizindikiro zina zambiri zozizwitsa pamaso pa ophunzira ake, zimene sizidalembedwe m'buku muno. Koma izi zalembedwa kuti mukhulupirire kuti Yesu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu, ndipo kuti pakukhulupirira mukhale ndi moyo m'dzina lake. Pambuyo pake Yesu adadziwonetsanso kwa ophunzira ake ku nyanja ya Tiberiasi. Adadziwonetsa motere: Simoni Petro, Tomasi (wotchedwa Didimo), Natanaele wochokera ku mudzi wa Kana m'dera la Galileya, ana aja a Zebedeo, ndiponso ophunzira ena aŵiri, anali pamodzi. Simoni Petro adaŵauza kuti, “Ine ndikukasodza.” Iwo adati, “Ifenso tipita nao.” Adanyamuka nakaloŵa m'chombo. Koma usiku umenewo sadaphe kanthu. Kutacha Yesu adaimirira pa mtunda. Komabe ophunzira aja sadazindikire kuti ndi Yesu. Tsono Iye adaŵafunsa kuti, “Kodi anzathu, mwaphako kanthu ngati?” Iwo adati, “Ai ndithu, tabwera chabe.” Yesu adaŵauza kuti, “Ponyani khoka ku dzanja lamanja la chombo, mupha kanthu.” Iwo adaponyadi, ndipo sadathe kulikokanso chifukwa cha kuchuluka kwa nsomba. Pamenepo wophunzira uja amene Yesu ankamukonda kwambiriyu adauza Petro kuti, “Ndi Ambuye!” Pamene Simoni Petro adamva kuti ndi Ambuye, adavala mkanjo wake (chifukwa anali atauvula), ndipo adadziponya m'nyanja. Koma ophunzira ena aja adadza ndi chombo ku mtunda akukoka khoka lodzaza ndi nsomba. Sanali kutali ndi mtunda, koma pafupi, ngati mamita 90. Pamene adafika pa mtunda, adaonapo moto wamakala, pali nsomba, ndiponso buledi. Yesu adaŵauza kuti, “Bwera nazoni nsomba zina zimene mwapha.” Apo Simoni Petro adaloŵa m'chombo muja nakokera khoka lija ku mtunda, lodzaza ndi nsomba zazikulu zokwanira 153. Ngakhale nsombazo zinali zochuluka chotero, khokalo silidang'ambike. Yesu adaŵauza kuti, “Bwerani, mufisule.” Koma mwa ophunzirawo panalibe ndi mmodzi yemwe amene adaalimba mtima kumufunsa kuti, “Ndinu yani?” Pakuti adaazindikira kuti ndi Ambuye. Yesu adadza natenga buledi uja nkuŵapatsa. Adateronso ndi nsomba zija. Aka nkachitatu kuti Yesu aonekere ophunzira ake Iye atauka kwa akufa. Iwo atafisula, Yesu adafunsa Simoni Petro kuti, “Iwe Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi koposa m'mene amandikondera aŵa?” Iye adati, “Inde Ambuye, mukudziŵa kuti ndimakukondani.” Yesu adamuuza kuti, “Samala anaankhosa anga.” Yesu adamufunsanso kachiŵiri kuti, “Iwe Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi?” Iye adati, “Inde Ambuye, mukudziŵa kuti ndimakukondani.” Yesu adamuuza kuti, “Ŵeta nkhosa zanga.” Yesu adamufunsa kachitatu kuti, “Iwe Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikonda?” Petro adayamba kumva chisoni kuti Yesu akumufunsa kachitatu kuti, “Kodi umandikonda?” Ndipo adati, “Ambuye, mumadziŵa zonse. Mukudziŵa kuti ineyo ndimakukondani.” Yesu adamuuza kuti, “Samala nkhosa zanga. Kunena zoona, pamene unali mnyamata, unkadzimanga wekha lamba nkumapita kulikonse kumene unkafuna kupita. Koma ukadzakalamba, udzatambalitsa manja ako, ndipo wina adzakumanga nkumapita nawe kumene sukufuna.” (Yesu adanena zimenezi pofuna kuŵadziŵitsa za m'mene Petro adzafere ndi kulemekeza Mulungu.) Atatero, adauza Petro kuti, “Unditsate.” Petro adacheuka, naona wophunzira uja amene Yesu ankamukonda kwambiri akuŵatsatira. Ndiye wophunzira yemwe uja amene adaatsamira pa chifukwa cha Yesu paphwando paja namufunsa kuti, “Ambuye, amene adzakuperekani kwa adani anu ndani?” Pamene Petro adamuwona iyeyo, adafunsa Yesu kuti, “Ambuye, nanga uyu bwanji?” Yesu adamuuza kuti, “Ngati ndifuna kuti iye akhalebe mpaka ndidzabwerenso, kodi iwe uli nazo kanthu? Iweyo unditsate.” Tsono mbiri idamveka pakati pa abale kuti wophunzira mnzaoyo sadzafa. Komatu Yesu sadamuuze kuti sadzafa ai, koma adaati, “Ngati ndifuna kuti iye akhalebe mpaka ndidzabwerenso, kodi iwe uli nazo kanthu?” Ameneyo ndiye wophunzira uja amene akuchitira umboni zimene zidachitikazo, ndipo ndiye amene adazilemba. Tikudziŵa kuti umboni wakewo ngwoona. Koma palinso zina zambiri zimene Yesu ankachita. Zikadalembedwa zonsezo, ndiganiza kuti pa dziko lonse lapansi sipakadaoneka malo okwanira mabuku onse olembedwawo. A Teofilo, M'buku langa loyamba lija ndidakulemberani za zonse zimene Yesu ankachita ndi kuphunzitsa kuyambira pa chiyambi, kufikira tsiku limene adatengedwa kupita Kumwamba. Mwa mphamvu ya Mzimu Woyera, anali atauza atumwi amene adaŵasankha aja zoti iwowo adzachite. Iye ataphedwa, adadziwonetsa wamoyo kwa iwo mwa njira zambiri zotsimikizika. Adaŵaonekera nalankhula nawo za ufumu wa Mulungu masiku makumi anai. Pamene anali nawo pamodzi, Yesu adaŵalamula kuti, “Musachoke mu Yerusalemu, koma mudikire mphatso imene Atate adalonjeza, monga ndidaakuuzani. Pajatu Yohane ankabatiza ndi madzi, koma pasanapite masiku ambiri, inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.” Tsono atumwi aja atasonkhana, adafunsa Yesu kuti, “Ambuye, kodi ino ndiyo nthaŵi yoti mukhazikitsenso ufumu mu Israele?” Iye adati, “Si ntchito yanu kuti mudziŵe nthaŵi kapena nyengo pamene zidzachitike zimene Atate adakhazikitsa mwa mphamvu yao. Koma mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera akadzabwera pa inu, ndipo mudzakhala mboni zanga ku Yerusalemu, ku Yudeya ndi ku Samariya konse, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.” Atanena zimenezi, Yesu adatengedwa kupita Kumwamba, iwo akupenya. Ndipo mtambo udamlandira nkumubisa, iwo osamuwonanso. M'mene atumwi aja ankayang'anitsitsabe kumwamba, Iye akupita, mwadzidzidzi anthu aŵiri ovala zoyera adaimirira pambali pao. Anthuwo adaŵafunsa kuti, “Inu anthu a ku Galileya, mwatani mwangoti chilili pamenepa mukuyang'ana kumwamba? Yesuyu amene watengedwa kuchokera pakati panu kupita Kumwamba, adzabweranso monga momwe mwamuwoneramu akupita Kumwambako.” Tsono atumwi aja adabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku Phiri la Olivi. Mtunda wake kuchokera ku Yerusalemu ngwosakwanira ngakhale mtunda umodzi. Ataloŵa mumzindamo, adakwera ku chipinda cham'mwamba kumene ankakhala: panali Petro, Yohane, Yakobe ndi Andrea; Filipo ndi Tomasi; Bartolomeo ndi Mateyo; Yakobe (mwana wa Alifeyo,) ndi Simoni (wa m'chipani chandale cha Azelote,) ndiponso Yudasi (mwana wa Yakobe.) Onseŵa ankalimbikira kupemphera ndi mtima umodzi, pamodzi ndi akazi ena, ndi Maria amai ake a Yesu, ndiponso abale ake a Yesu. Tsiku lina, patapita masiku angapo, Petro adaimirira pakati pa abale. (Anthuwo onse pamodzi anali ngati 120.) Iye adati, “Abale anga, kunayenera kuti zichitikedi zimene Malembo adaneneratu za Yudasi. Paja kudzera mwa Davide Mzimu Woyera adalankhula za iyeyo amene adatsogolera anthu okagwira Yesu. Yudasiyo anali mmodzi wa gulu lathu, ndipo adaalandira udindo woti azitumikira pamodzi ndi ife. Adagula munda ndi ndalama zimene adapata pochita chosalungama chija. Kumeneko adagwa chamutu, naphulika pakati, matumbo ake onse nkukhuthuka. Anthu onse okhala ku Yerusalemu adamva zimenezi, kotero kuti m'chilankhulo chao mundawo adautcha dzina loti ‘Akeledama,’ ndiye kuti, ‘Munda wa Magazi.’ Paja m'buku la Masalimo muli mau akuti, “ ‘Nyumba yake isanduke bwinja, pasakhale munthu wogonamo.’ Muli mau enanso akuti, “ ‘Wina alandire ntchito yake.’ “Pali anthu ena amene akhala akutsagana nafe nthaŵi yonse pamene Ambuye Yesu anali pakati pathu, kuyambira pamene Iye adabatizidwa ndi Yohane mpaka tsiku limene adatengedwa kuchoka pakati pathu kupita Kumwamba. Mmodzi mwa anthu ameneŵa akhale mboni pamodzi ndi ife, yakuti Yesu adauka kwa akufa.” Pamenepo iwo adatchula maina aŵiri: Yosefe amene ankamutcha Barsabasi (dzina lake lina ndi Yusto,) ndi Matiasi. Ndipo adapemphera kuti, “Ambuye, Inu amene mumadziŵa mitima ya anthu onse, tiwonetseni ndi uti mwa aŵiriŵa amene mwamusankha kuti alandire ntchito iyi ya utumwi, m'malo mwa Yudasi uja amene adaisiya ndipo adapita ku malo omuyenera.” Tsono adaŵachitira maere anthu aŵiriwo. Maerewo adagwera Matiasi, ndipo iyeyo adawonjezedwa pa gulu lija la atumwi khumi ndi mmodzi. Pamene tsiku la chikondwerero cha Pentekoste lidafika, iwo onse anali pamodzi m'nyumba imodzi. Mwadzidzidzi kudamveka kuchokera kumwamba mkokomo ngati wa mphepo yaukali, nudzaza nyumba yonse imene ankakhalamo. Ndipo adaona ngati timalaŵi ta moto tooneka ngati malilime tikugaŵikana nkukhala pa iwo, aliyense kakekake. Onse aja adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo adayamba kulankhula zilankhulo zachilendo, monga Mzimuyo ankaŵalankhulitsira. Tsono, m'Yerusalemu muja munali Ayuda ena, anthu okonda Mulungu, ochokera ku maiko onse a pa dziko lapansi. Pamene mkokomo uja udamveka, anthu ambirimbiri adasonkhana. Onse adadodoma, chifukwa aliyense mwa iwo ankaŵamva akulankhula chilankhulo chake. Adadabwa, nathedwa nzeru ndipo adati, “Kodi onse akulankhulaŵa, si Agalileya? Nanga bwanji aliyense mwa ife akuŵamva akulankhula chilankhulo chakwao? Ena mwa ife ndi Aparti ndi Amedi ndi Aelami, ena ndi okhala ku Mesopotamiya, ku Yudeya ndi ku Kapadokiya, ku Ponto ndi ku Asiya, ku Frijiya ndi ku Pamfiliya, ku Ejipito, ndi ku madera a Libiya kufupi ndi ku Kirene, ena ndi alendo ochokera ku Roma, ndiye kuti Ayuda ndi ena otsata za Chiyuda. Enanso ndi Akrete ndi Aarabu, komabe tonse tikuŵamva anthuŵa akulankhula m'zilankhulo zathu za ntchito zazikulu za Mulungu.” Onse adazizwa ndi kuthedwa nzeru, ndipo adayamba kufunsana kuti, “Kodi chimenechi nchiyani?” Koma ena ankangoseka nkumati, “Aledzera vinyo watsopano.” Koma Petro adaimirira pamodzi ndi atumwi ena aja khumi ndi mmodzi, ndipo iye adanena mokweza mau kuti, “Inu Ayuda, ndi inu nonse okhala ku Yerusalemu kuno, tamverani ndipo mumvetsetse bwino mau anga. Anthuŵa sadaledzere ai, monga mukuganizira inu, pakuti nthaŵi idakali 9 koloko m'maŵa. Koma zimenezi ndi zomwe mneneri Yowele adalosa kuti, “ ‘Mulungu akuti, Pa masiku otsiriza ndidzaika Mzimu wanga mwa anthu onse, ndipo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi azidzalalika za Mulungu. Anyamata anu azidzaona zinthu m'masomphenya, ndipo nkhalamba zanu zizidzalota maloto. Ndithu, pa masiku amenewo ndidzaika Mzimu wanga ngakhale mwa akapolo anga aamuna ndi aakazi, ndipo azidzalalika za Mulungu. Ndidzachita zozizwitsa ku thambo lakumwamba, ndipo pansi pano zizindikiro izi: magazi, moto ndi utsi watolotolo. Dzuŵa lidzangoti bii ngati mdima ndipo mwezi udzangoti psuu ngati magazi, lisanafike tsiku la Ambuye Mulungu lalikulu ndi laulemerero. Pamenepo aliyense amene adzatama dzina la Ambuye mopemba, adzapulumuka.’ “Inu Aisraele mverani mau aŵa. Yesu wa ku Nazarete anali munthu amene Mulungu adamtuma kwa inu. Mulungu adakutsimikizirani zimenezi ndi zamphamvu, zozizwitsa ndi zizindikiro zimene ankachita kudzera mwa Iyeyo pakati panu, monga mukudziŵa. Tsono Yesuyo adaperekedwa monga momwe Mulungu adaakonzeratu, ndi m'mene Iye amadziŵiratu zinthu. Ndipo inuyo mudamupha pakumpereka kwa anthu ochimwa kuti ampachike pa mtanda. Koma Mulungu adammasula ku zoŵaŵa za imfa, namuukitsa kwa akufa, chifukwa kunali kosatheka kuti agonjetsedwe ndi imfa. “Paja Davide ponena za Iye adati, ‘Ndinkaona Ambuye Mulungu pamaso panga nthaŵi zonse, pakuti amakhala ku dzanja langa lamanja kuti ndingagwedezeke. Nchifukwa chake mtima wanga udakondwa, ndipo ndinkalankhula mosangalala. Ndithu, ngakhale thupi langa lomwe lidzapumula m'manda, ndikhulupirira kuti simudzandisiya ku Malo a anthu akufa, kapena kulekerera Woyera wanu kuti aole. Mudandidziŵitsa njira zopita ku moyo, ndipo mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu.’ “Abale anga, ndingathe kulankhula nanu monenetsa za kholo lathu Davide. Iye adamwalira, naikidwa m'manda, ndipo manda ake alipo mpaka pano. Paja iye anali mneneri, ndipo ankadziŵa zimene Mulungu adamlonjeza molumbira zakuti mmodzi mwa zidzukulu zake ndiye adzaloŵe ufumu wake. Ndiye kuti Davideyo adaaoneratu zimenezi, zakuti Khristu adzauka kwa akufa, ndipo pamenepo adanena mau aja akuti, “ ‘Iye sadasiyidwe ku Malo a anthu akufa, ndipo thupi lake silidaole.’ Yesu yemweyo Mulungu adamuukitsadi kwa akufa, ndipo tonsefe ndife mboni za zimenezi. Iye adakwezedwa kukakhala ku dzanja lamanja la Mulungu, nalandira Mzimu Woyera, amene Atate adaalonjeza. Ndipo zimene mukuwona ndi kumvazi ndiye mphatso yake imene watitumizira. Pajatu Davide sadakwere kupita Kumwamba, koma iye yemwe adati, “ ‘Ambuye adauza Mbuye wanga kuti, Khala ku dzanja langa lamanja mpaka ndisandutse adani ako kuti akhale ngati chopondapo mapazi ako.’ “Tsono Aisraele onse adziŵe ndithu kuti Yesu uja inu mudampachika pamtandayu, Mulungu adamsankhula kuti akhale Ambuye ndi Mpulumutsi.” Pamene anthu aja anamva zimenezi, zidaŵalasa mtima, ndipo adafunsa Petro ndi atumwi ena aja kuti, “Abale, tsono ifeyo tichite chiyani?” Petro adaŵauza kuti, “Tembenukani mtima, ndipo aliyense mwa inu abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Mukatero machimo anu akhululukidwa, ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera. Paja zimene Mulungu adalonjeza zija, adalonjezera inuyo, ana anu ndiponso anthu onse okhala kutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaŵaitana.” Petro adalankhulanso mau ena ambiri, naŵachenjeza kuti, “Muthaŵe maganizo opotoka a mbadwo woipa uno.” Pamenepo anthu amene adamvera mau akewo adabatizidwa, ndipo tsiku limenelo anthu ngati zikwi zitatu adaonjezedwa pa gulu lao. Anthuwo ankasonkhana modzipereka kuti amve zimene atumwi ankaphunzitsa. Ankayanjana, ndipo ankadya Mgonero wa Ambuye ndi kupemphera pamodzi. Anthu onse ankaopa Mulungu poona zozizwitsa ndi zizindikiro zambiri zimene atumwi ankachita. Okhulupirira onse anali amodzi, ndipo ankagaŵana zinthu zao. Ankagulitsa minda yao ndi katundu wao, ndalama zake nkumagaŵira onse, malinga ndi kusoŵa kwa aliyense. Tsiku ndi tsiku ankasonkhana ndi mtima umodzi m'Nyumba ya Mulungu, ndipo ankadyera pamodzi kunyumba kwao. Ankadya chakudya chaocho mosangalala ndiponso ndi mtima waufulu. Ankatamanda Mulungu, ndipo anthu onse ankaŵakomera mtima. Ndipo tsiku ndi tsiku Ambuye ankaŵawonjezera ena olandira chipulumutso. Tsiku lina Petro ndi Yohane ankapita ku Nyumba ya Mulungu pa 3 koloko madzulo, nthaŵi ya mapemphero. Anthu ena adaanyamula munthu wina wopunduka miyendo chibadwire. Masiku onse ankamuika pa khomo la Nyumba ya Mulungu lotchedwa “Khomo Lokongola,” kuti iye azipempha kwa anthu oloŵa m'Nyumbamo. Pamene iye adaona Petro ndi Yohane akuloŵa m'Nyumba ya Mulungu, adaŵapempha kuti ampatseko kanthu. Iwo adampenyetsetsa, ndipo Petro adamuuza kuti, “Tatiyang'ana” Iye nkuŵayang'anadi namaganiza kuti alandira kanthu kwa iwo. Koma Petro adamuuza kuti, “Ndalama ndilibe, koma ndikupatsa chimene ndili nacho: m'dzina la Yesu Khristu wa ku Nazarete, yenda!” Atatero adamgwira dzanja lamanja, namuimiritsa. Pompo mapazi ake ndi akakolo ake adalimba. Adalumpha, naimirira, nayamba kuyenda, ndipo adaloŵa nao m'Nyumba ya Mulungu akuyenda ndi kulumpha ndi kutamanda Mulungu. Anthu onse adamuwona akuyenda ndi kutamanda Mulungu. Adamzindikira kuti ndi yemwe uja amene ankakhala pa Khomo Lokongola la Nyumba ya Mulungu. Ndipo adazizwa ndithu ndi kudabwa ndi zimene zidamchitikira. Munthu uja adaakangamira Petro ndi Yohane, ndipo anthu onse adadabwa, naŵathamangira ku Khonde lotchedwa Khonde la Solomoni. Pamene Petro adaona zimenezi, adalankhula nawo anthuwo, adati, “Inu Aisraele, bwanji mukuzizwa ndi zimenezi? Bwanji mukutiyang'ana ngati kuti tamuyendetsa munthuyu ndi mphamvu zathuzathu? Kodi mukuyesa kuti nchifukwa choti ndife opembedza Mulungu kopambana? Iyai, koma Mulungu wa makolo athu, Abrahamu, Isaki ndi Yakobe, adapereka ulemerero kwa Yesu, Mtumiki wake. Inu mudampereka kwa adani ake ndi kumkana pamaso pa Pilato, pamene Pilatoyo adaatsimikiza kuti ammasula. Yesu anali woyera mtima ndi wolungama, koma inu mudamkana, ndipo m'malo mwake mudapempha kuti akumasulireni chigaŵenga. Mudapha Wopatsa moyo, koma Mulungu adamuukitsa kwa akufa. Ife ndife mboni za zimenezi. Munthuyu, amene mukumuwona ndipo mukumdziŵa, wakhulupirira dzina la Yesu. Chikhulupirirocho chimene ali nacho mwa Yesu, ndicho chalimbitsa miyendo yake, chamchiritsa kwenikweni, monga inu nonse mukuwoneramu. “Ndiponso tsopano abale anga, ndikudziŵa kuti inu ndi akuluakulu anu mudachita zimenezi mosadziŵa. Koma Mulungu adaaneneratu mwa aneneri onse kuti Wodzozedwa wake wolonjezedwa uja adzamva zoŵaŵa, ndipo zidachitikadi momwemo. Tsono tembenukani mtima ndi kubwerera kwa Mulungu, kuti akufafanizireni machimo anu. Motero Ambuye adzakupatsani nthaŵi ya mpumulo, ndipo adzakutumizirani Yesu uja amene adamusankhuliratu kuti akhale Mpulumutsi wanu. Iyeyo anayenera kukhala Kumwamba mpaka nthaŵi yakukonza zonse kwatsopano, monga Mulungu adanenera kuyambira kalekale mwa aneneri ake oyera mtima. Paja Mose adati, ‘Ambuye Mulungu adzasankhula mmodzi pakati pa abale anu, kuti akhale Mneneri wanu monga ine. Mudzamvere zonse zimene Iye adzakuuzeni. Aliyense amene sadzamvera Mneneriyo, amchotseretu mwa Aisraele ndi kumuwononga.’ Ndipo aneneri onse amene adalankhula, kuyambira Samuele, mpaka onse amene adadza pambuyo pake, ankalalika za masiku omwe ano. Zimene Mulungu adalonjeza kudzera mwa aneneri nzokhudza inuyo ana ao. Momwemonso chipangano chimene adachita ndi makolo anu chikukhudza inu ana ake. Paja adauza Abrahamu kuti, ‘Mwa chidzukulu chako china ndidzadalitsa mitundu yonse ya anthu a pa dziko lapansi.’ Choncho Mulungu atasankhula Mtumiki wake adayamba kumtuma kwa inu, kuti akudalitseni pakuthandiza aliyense mwa inu kusiya njira zake zoipa.” Petro ndi Yohane akulankhulabe ndi anthu aja, kudadza ansembe ena pamodzi ndi mkulu wa asilikali a ku Nyumba ya Mulungu, ndi Asaduki. Iwoŵa anali okwiya chifukwa chakuti atumwi aŵiriwo ankaphunzitsa anthu ndi kulalika kuti, “Popeza kuti Yesu adauka kwa akufa, ndiye kuti akufa adzaukanso.” Tsono adaŵagwira, ndipo poti kunali kutada kale, adaŵaika m'ndende kufikira m'maŵa. Koma ambiri mwa anthu amene adamva mau aja a atumwi adakhulupirira. Chiŵerengero cha okhulupirirawo chidaakwanira ngati zikwi zisanu. M'maŵa mwake atsogoleri a Ayuda, akulu ao, ndiponso aphunzitsi a Malamulo adasonkhana ku Yerusalemu. Kunalinso Anasi mkulu wa ansembe onse, pamodzi ndi Kayafa, Yohane, Aleksandro ndi ena onse a kubanja kwa mkulu wa ansembe onse. Tsono adaimiritsa Petro ndi Yohane pakati pao naŵafunsa kuti, “Kodi zija mudachitazi, mudazichita ndi mphamvu yanji, kaya mudazichita m'dzina la yani?” Petro, atadzazidwa ndi Mzimu Woyera, adaŵayankha kuti, “Inu atsogoleri ndi akuluakulu muli apa, kodi mukutifunsa ife lero za ntchito yabwino imene idachitika pa munthu wopunduka uja, ndi kuchira kwake? Mudziŵetu tsono inu nonse, ndi Aisraele ena onse, kuti munthuyu akuima wamoyo pamaso panu chifukwa cha mphamvu ya dzina la Yesu Khristu wa ku Nazarete. Amene uja inu mudaampachika pa mtanda, koma Mulungu adamuukitsa kwa akufa. Za Yesuyo mau a Mulungu akuti, “ ‘Mwala umene inu amisiri omanga nyumba mudaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya, wofunika koposa.’ Ndipo palibe wina aliyense amene angathe kupulumutsa anthu, pakuti pa dziko lonse lapansi palibe dzina lina limene Mulungu adapatsa anthu kuti tipulumuke nalo.” Abwalo aja adazizwa poona kulimba mtima kwa Petro ndi Yohane, ndiponso podziŵa kuti anali anthu wamba, osaphunzira kwambiri. Apo adazindikira kuti anali anzake a Yesu. Tsono poonanso munthu wochiritsidwa uja ataimirira pafupi ndi Petro ndi Yohane, adasoŵa poŵatsutsira. Choncho adaŵalamula kuti atuluke m'bwalo la milandu lija, kenaka abwalowo adayamba kukambirana. Adati, “Kodi tiŵachite chiyani anthu ameneŵa? Pajatu anthu onse okhala m'Yerusalemu muno akudziŵa kuti iwoŵa adachitadi chizindikiro chozizwitsa, ndipo ife zimenezo sitingathe kukana. Koma kuwopa kuti mbiriyi ingaŵande ponseponse, tiyeni tiwachenjeze moopseza kuti polankhula ndi munthu aliyense asatchulenso dzina la Yesu.” Atatero adaŵaitana, naŵalamula kuti asatchule konse kapena kuphunzitsa za dzina la Yesu. Koma Petro ndi Yohane adaŵayankha kuti, “Weruzani nokha, kodi pamaso pa Mulungu nkwabwino kumvera inuyo koposa kumvera Mulunguyo? Ife ndiye sitingaleke kulankhula za zimene tidaziwona ndi kuzimva.” Abwalowo adaŵachenjezanso moopseza koposa kale, naŵamasula. Sadapeze njira yoti nkuŵalangira, popeza kuti anthu onse ankatamanda Mulungu chifukwa cha zimene zidaachitikazo. Ndipo munthu wochiritsidwa mododometsayo anali wa zaka zopitirira makumi anai. Petro ndi Yohane atamasulidwa, adapita kwa anzao naŵasimbira zonse zimene akulu a ansembe ndi akulu ena a Ayuda adaaŵauza. Pamene iwo adamva zimenezi, onse adayamba kupemphera ndi mtima umodzi. Adati, “Ambuye, ndinu amene mudalenga dziko lakumwamba, dziko lapansi, nyanja, ndi zonse zili m'menemo. Mwa Mzimu Woyera mudalankhulitsa kholo lathu Davide, mtumiki wanu, pamene adati, “ ‘Chifukwa chiyani anthu akunja adakalipa, anthu a mitundu ina adaganiziranji zopandapake? Mafumu a dziko lapansi adakonzekera, akulu a Boma adasonkhana pamodzi kulimbana ndi Chauta, ndiponso ndi wodzozedwa wake uja?’ “Zoonadi, Herode ndi Ponsio Pilato adasonkhana mumzinda muno pamodzi ndi anthu akunja, ndiponso ndi anthu a Israele, kuti alimbane ndi Yesu, Mtumiki wanu wopatulika amene mudamdzoza. Motero iwo adachitadi zonse zija zimene Inu mudaakonzeratu kale mwa mphamvu zanu ndi nzeru zanu kuti zichitike. Ndiye tsono Ambuye, onani zimene akutiwopsezazi, ndipo mutithandize atumiki anufe, kuti tilankhule mau anu molimba mtima ndithu. Tambalitsani dzanja lanu kuti anthu achire, ndipo pachitike zizindikiro ndi zozizwitsa m'dzina la Mtumiki wanu wopatulika.” Atatha kupemphera, nyumba imene adasonkhanamo ija idayamba kugwedezeka. Onse adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula mau a Mulungu molimba mtima. Gulu lonse la okhulupirira linali la mtima umodzi, ndi la maganizo amodzi. Panalibe munthu amene ankati, “Zimene ndiri nazo nzangazanga,” koma aliyense ankapereka zake zonse kuti zikhale za onse. Atumwi ankachita umboni ndi mphamvu yaikulu kuti Ambuye Yesu adaukadi kwa akufa, ndipo onse Mulungu ankaŵakomera mtima kwambiri. Panalibe munthu wosoŵa kanthu pakati pao, chifukwa onse amene anali ndi minda kapena nyumba, ankazigulitsa, namabwera ndi ndalama zake kudzazipereka kwa atumwi. Ndipo ndalamazo ankagaŵira munthu aliyense malinga ndi kusoŵa kwake. Panali munthu wina dzina lake Yosefe, wa fuko la Levi, mbadwa ya ku Kipro, amene atumwi adaamutcha Barnabasi, ndiye kuti Wolimbitsa mtima. Nayenso adagulitsa munda wake, nabwera ndi ndalama zake kudzazipereka kwa atumwi. Munthu winanso, dzina lake Ananiya, pamodzi ndi mkazi wake Safira, adagulitsa munda wao. Mopangana ndi mkazi wake, adapatulapo ndalama zina za mundawo, nakapereka zotsala kwa atumwi. Koma Petro adamufunsa kuti, “Iwe Ananiya, chifukwa chiyani walola mtima wako kugwidwa ndi Satana mpaka kumanamiza Mzimu Woyera pakupatula ndalama zina za munda wako? Usanaugulitse, sunali wako kodi? Ndipo utaugulitsa, suja ndalama zake zinali m'manja mwako? Nanga udalola bwanji zoterezi mumtima mwako? Pamenepatu sudanamize anthu, koma wanamiza Mulungu.” Pamene Ananiya adamva mau ameneŵa, adagwa pansi, naafa pomwepo. Ndipo anthu onse amene adamva zimenezi adachita mantha aakulu. Tsono achinyamata adabwera namkulunga m'nsalu. Adamnyamula nakamuika m'manda. Patapita ngati maora atatu, mkazi wake adaloŵa, osadziŵa zimene zachitika. Petro adamufunsa kuti, “Tandiwuzani, kodi pogulitsa munda wanu, mtengo wake unali ndalama izi?” Maiyo adati, “Inde, mtengo wake unali womwewo.” Tsono Petro adamufunsa kuti, “Bwanji mudapangana kuyesa Mzimu wa Ambuye? Ndipotu anthu amene akaika mwamuna wanu ndi aŵa ali pakhomoŵa, akunyamulani inunso.” Pomwepo adagwa pansi ku mapazi a Petro, naafa. Pamene achinyamata aja adaloŵa, adampeza atafa kale. Adamnyamula nakamuika pafupi ndi mwamuna wake. Ndipo mpingo wonse ndi anthu onse amene adamva zimenezi, adagwidwa ndi mantha aakulu. Atumwi ankachita zizindikiro ndi zozizwitsa zambiri pakati pa anthu. Onse okhulupirira Khristu ankasonkhana ndi mtima umodzi m'Khonde la Solomoni. Mwa anthu enawo panalibe ndi mmodzi yemwe amene adaalimba mtima kuti azisonkhana nawo, komabe anthu onse ankaŵatama. Ndipo anthu okhulupirira Ambuye ankachulukirachulukira, mwakuti linali ndithu gulu lalikulu la amuna ndi akazi omwe. Tsono anthu ankatulutsira odwala ao m'miseu yamumzinda, nkumaŵagoneka pa mabedi ndi pa mphasa, kuti Petro podutsapo, chithunzithunzi chake chokha ena mwa iwo chiŵafike. Kunkasonkhananso anthu ochuluka ochokera ku midzi yozungulira Yerusalemu. Anali atanyamula anthu odwala, ndiponso ena osautsidwa ndi mizimu yoŵaipitsa. Onsewo ankachiritsidwa. Pamenepo mkulu wa ansembe onse pamodzi ndi anzake aja, ndiye kuti a m'chipani cha Asaduki, onsewo adadukidwa nazo. Tsono adagamula zochitapo kanthu. Adagwira atumwi aja, naŵatsekera m'ndende ya Boma. Koma usiku mngelo wa Ambuye adatsekula zitseko za ndendeyo naŵatulutsa. Adaŵauza kuti, “Pitani m'Nyumba ya Mulungu muzikauza anthu mau onse okhudza za moyo watsopanowu.” Atumwi aja adamveradi zimenezi, adakaloŵa m'Nyumba ya Mulungu m'mamaŵa, nayamba kuphunzitsa. Pamene mkulu wa ansembe onse adafika pamodzi ndi anzake aja, adaitanitsa msonkhano wa Bungwe Lalikulu, ndiye kuti Bwalo lonse la akuluakulu a Aisraele. Tsono adatuma anthu kuti apite ku ndende akaŵatenge atumwi aja. Koma pamene anthuwo adafika kundendeko, sadaŵapezemo. Adabwerako nadzaŵafotokozera. Adati, “Takapeza ndende ili chitsekere ndithu, ndipo alonda ali chilili pa makomo, koma titatsekula zitseko, sitidapezemo munthu.” Pamene mkulu wa asilikali a ku Nyumba ya Mulungu ndi akulu a ansembe adamva mau ameneŵa, adatha nawo nzeru, osadziŵa kwachitika zotani. Koma munthu wina adadzaŵauza kuti, “Anthu amene mudaŵatsekera m'ndende aja, ali m'Nyumba ya Mulungu ndipo akuphunzitsa anthu.” Pamenepo mkulu wa asilikali uja pamodzi ndi asilikaliwo adapita nkukaŵatenga atumwiwo. Sadaŵatenge mwankhondo ai, chifukwa ankaopa kuti anthu angaŵaponye miyala. Atafika nawo, adaŵakhazika pamaso pa Bungwe Lalikulu lija, ndipo mkulu wa ansembe onse adayamba kuŵafunsa mafunso. Adati, “Paja tidakuletsani mwamphamvu kuti musaphunzitse konse m'dzina la Yesu, koma inu mwafalitsa zophunzitsa zanuzo m'Yerusalemu monse, ndipo mukufuna kusenzetsa ife imfa ya munthu ameneyu.” Koma Petro ndi atumwi enawo adati, “Tiyenera kumvera Mulungu koposa kumvera anthu. Mulungu wa makolo athu adaukitsa Yesu kwa akufa, Iye amene inu mudaamupha pakumpachika pa mtanda. Ameneyo Mulungu adamkweza ku dzanja lake lamanja kuti akhale Mtsogoleri ndi Mpulumutsi. Adachita zimenezi kuti apatse Aisraele mwai wotembenuka mtima kuti machimo ao akhululukidwe. Mboni za zimenezi ndi ifeyo ndiponso Mzimu Woyera amene Mulungu adampereka ngati mphatso kwa anthu omvera Iye.” Pamene abwalo aja adamva zimenezi, adakwiya kwambiri nafuna kuŵapha. Koma wina mwa iwo, Mfarisi dzina lake Gamaliele, mphunzitsi wa Malamulo, amene anthu onse ankamlemekeza, adaimirira. Adalamula kuti anthu aja abaapita panja. Tsono adauza abwalowo kuti, “Inu Aisraele, chenjerani ndi zimene mukufuna kuŵachita anthuŵa. Pajatu si kale pamene munthu wina dzina lake Teudasi adaabwera nkuyesa kudzimveketsa, ndipo anthu ngati mazana anai adamtsata. Iye uja adaphedwa, ndipo anthu onse amene ankamtsata aja adabalalikana natheratu. Pambuyo pake, pa nthaŵi ya kalembera, padabweranso wina dzina lake Yudasi, wa ku Galileya, nakopa anthu ambiri kuti amtsate. Iyenso adaphedwa, ndipo anthu onse amene ankamtsata aja adabalalikana. Nchifukwa chake pa nkhani imeneyi ndikukuuzani kuti, muŵaleke anthuŵa, ndipo muŵalole azipita. Ngati zimene iwo akuganiza ndiponso zimene akuchitazi nzochokera kwa anthu, zidzakanika zokha. Koma ngati nzochokera kwa Mulungu, inu simungathe kuŵaletsa ai. Mwina mungapezeke kuti mukulimbana ndi Mulungu.” Abwalowo adavomerezana naye, naŵaitana atumwi aja. Adaŵakwapula, naŵaletsa kuti asalankhulenso m'dzina la Yesu, kenaka adaŵalola kuti apite. Iwo adachoka kubwaloko ali okondwa kuti Mulungu waŵaŵerengera ngati oyenera kunyozeka chifukwa cha dzina la Yesu. Tsono tsiku ndi tsiku ankaphunzitsabe ndi kulalika m'Nyumba ya Mulungu ndi m'nyumba za anthu, Uthenga Wabwino wakuti Yesu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja. Masiku amenewo ophunzira aja ankachulukirachulukira. Koma Ayuda olankhula Chigriki anali ndi dandaulo pa Ayuda olankhula Chiyuda kuti akazi ao amasiye sankasamalidwa bwino pamene zachifundo za tsiku ndi tsiku zinkagaŵidwa. Tsono atumwi khumi ndi aŵiri aja adasonkhanitsa gulu lonse la ophunzira, naŵauza kuti, “Sibwino kuti ife tizisiya kulalika mau a Mulungu nkumayang'anira za chakudya. Nchifukwa chake abale, pakati panupa sankhanipo amuna asanu ndi aŵiri, a mbiri yabwino, odzazidwa ndi Mzimu Woyera ndiponso ndi nzeru. Tidzapatsa iwowo ntchitoyi. Koma ife tidzadzipereka ku ntchito ya kupemphera ndi kulalika mau a Mulungu.” Mau ameneŵa adakomera gulu lonse lija, motero adasankha Stefano, munthu wodzazidwa ndi chikhulupiriro ndiponso ndi Mzimu Woyera. Adasankhanso Filipo, Prokoro, Nikanore, Timoni, Parmenasi, ndi Nikolasi wa ku Antiokeya, yemwe kale anali atasiya chikunja kutsata chiyuda. Adaŵaimiritsa pamaso pa atumwi, ndipo atumwiwo adapemphera naŵasanjika manja. Mau a Mulungu ankafalikira ponseponse, ndipo ophunzira ankachulukirachulukira ndithu ku Yerusalemu. Ansembe omwe ambirimbiri ankamvera chikhulupirirocho. Stefano anali munthu amene Mulungu adamkomera mtima kwambiri namdzaza ndi mphamvu, kotero kuti ankachita zizindikiro zozizwitsa pakati pa anthu. Koma kudabwera anthu ena a ku Kirene ndi a ku Aleksandriya, a ku nyumba yamapemphero yotchedwa “Nyumba Yamapemphero ya Opatsidwa Ufulu.” Iwoŵa pamodzi ndi ena a ku Silisiya ndi a ku Asiya adayamba kutsutsana ndi Stefano. Koma adalephera kumgonjetsa, chifukwa iye ankalankhula ndi nzeru zochokera kwa Mzimu Woyera. Tsono iwo adapangira anthu ena kuti azinena kuti, “Tidamumva akunyoza mwachipongwe Mose ndi Mulungu yemwe.” Motero adautsa mitima ya anthu, ya akuluakulu ao, ndiponso ya aphunzitsi a Malamulo. Iwoŵa adamuukira Stefano, namgwira, nkupita naye ku Bungwe Lalikulu la Ayuda. Adaimiritsa mboni zonama, izozo zidati, “Munthu uyu amangokhalira kulankhula mau onyoza Nyumba ya Mulungu ndiponso Malamulo a Mose. Tidamumva iyeyu akunena kuti Yesu wa ku Nazarete uja adzaononga malo ano, ndipo adzasintha miyambo imene Mose adatipatsa.” Ndipo onse amene anali m'Bungwemo adapenyetsetsa Stefanoyo, naona kuti nkhope yake inali ngati nkhope ya mngelo. Mkulu wa ansembe onse adafunsa Stefano kuti, “Kodi zimenezi nzoona?” Iye adayankha kuti, “Abale anga ndi atate anga, mverani! Mulungu waulemerero adaonekera kholo lathu Abrahamu pamene ankakhala ku Mesopotamiya, asanakakhale ku Harani. Adamuuza kuti, ‘Tuluka m'dziko lako, uŵasiye abale ako, ubwere ku dziko limene ndidzakusonyeza.’ Tsono adatulukadi m'dziko la Akaldeya nakakhala ku Harani. Bambo wake atamwalira, Mulungu adamchotsa kumeneko, nakamufikitsa ku dziko lino kumene inu mukukhala tsopano. Mulungu sadampatseko ndi kadera kakang'onong'ono komwe ka dzikoli kuti kakhale kakekake. Koma adamlonjeza kuti adzampatsa dzikoli kuti likhale lakelake ndiponso la zidzukulu zake, ngakhale pa nthaŵi imeneyo nkuti akadalibe mwana. Mulungu adati, ‘Zidzukulu zako zidzakhala alendo ku dziko lina kumene eniake adzaziyesa akapolo, nadzazizunza pa zaka mazana anai.’ Mulungu adatinso, ‘Koma Ine ndidzaulanga mtundu wa anthuwo umene udzazisandutsa akapolo. Bwino lake zidzatuluka m'dzikomo nkudzandipembedza pamalo pano.’ Tsono Mulungu adachita chipangano ndi Abrahamu, chimene chizindikiro chake chinali kuumbala. Motero Abrahamu adaumbala mwana wake Isaki, ali ndi masiku asanu ndi atatu akubadwa. Isaki adaumbala Yakobe, ndipo Yakobe adaumbala makolo athu khumi ndi aŵiri aja. “Tsono makolo athuwo adachita nsanje ndi mbale wao Yosefe, ndipo adamgulitsa kuti akakhale kapolo ku Ejipito. Koma Mulungu anali naye, mwakuti adampulumutsa ku masautso ake onse. Adampatsa nzeru ndi kumkometsa pamaso pa Farao, mfumu ya ku Ejipito, kotero kuti mfumuyo idamuika kuti akhale nduna yaikulu ya dziko la Ejipito, ndiponso woyang'anira banja lake lonse. Koma mudadzaloŵa njala m'dziko lonse la Ejipito, ndiponso m'Kanani, kotero kuti anthu adazunzika kwambiri. Makolo athu omwe sadathe kupeza chakudya. Pamene Yakobe adamva kuti ku Ejipito kuli tirigu, adatumako makolo athu aja. Uwu unali ulendo wao woyamba. Pa ulendo wachiŵiri Yosefe adadziwulula kwa abale akewo, ndipo adadziŵitsa Farao za banja lonselo. Tsono Yosefe adaitanitsa Yakobe, bambo wake, pamodzi ndi banja lake lonse. Onse pamodzi anali anthu 75. Motero Yakobe adapita ku Ejipito, iye ndi makolo athu omwe aja. Onsewo adakamwalira kumeneko. Pambuyo pake iye adaŵanyamula kupita nawo ku Sekemu, kumene adaŵaika m'manda amene Abrahamu adaagula ndi ndalama kwa ana a Hamori ku Sekemu. “Pamene idayandikira nthaŵi yakuti Mulungu achite zimene adaalonjeza kwa Abrahamu, mtundu wathu udakula ndi kuchuluka ku Ejipito. Pambuyo pake mfumu ina imene sidadziŵe Yosefe, idayamba kulamulira ku Ejipito. Mfumuyo idachenjerera mtundu wathu, nkuyamba kuzunza makolo athu, pakuŵatayitsa ana ao akhanda kuti asakhale ndi moyo. Nthaŵi imeneyo Mose adabadwa, ndipo anali mwana wokongola kwambiri. Adamlera kwao miyezi itatu, koma atamsiya pamtsinje paja, mwana wamkazi wa Farao adamtola, namlera ngati mwana wake. Motero Mose adaphunzira nzeru zonse za anthu a ku Ejipito, ndipo mau ake ndi ntchito zake zinali zamphamvu. “Pamene zaka zake zidafikira makumi anai, adaganiza zokayendera abale ake, Aisraele. Tsono pamene adaona kuti Mwejipito wina akuzunza mmodzi mwa abale akewo, Moseyo adatchinjiriza Mwisraeleyo, nalipsira Mwejipito uja pakumupha. Iye ankaganiza kuti abale ake adzazindikira kuti Mulungu adamuika kuti adzaŵapulumutse, koma iwo sadazindikire. M'maŵa mwake atabwera, adapeza Aisraele aŵiri akumenyana. Adayesa kuŵayanjanitsa pakuŵauza kuti, ‘Anthuni, muli pa chibale, bwanji mukuvutana?’ Koma amene adaaputa mnzakeyo adakankhira Mose kumbali nati, ‘Adakuika ndani kuti ukhale mkulu wathu ndi muweruzi wathu? Kodi ukufuna kuphanso ine monga udaphera Mwejipito dzulo lija?’ Pamene Mose adamva mau ameneŵa, adathaŵa namakakhala ku chilendo ku dziko la Midiyani. Kumeneko adabereka ana aamuna aŵiri. “Tsono patapita zaka makumi anai, mngelo adaonekera Mose ku chipululu cha ku phiri la Sinai, m'malaŵi a moto pa chitsamba. Mose ataona zimenezi adazizwa, ndipo adasendera pafupi kuti aonetsetse. Pamenepo adamva mau a Chauta akuti, ‘Ine ndine Mulungu wa makolo ako, Mulungu wa Abrahamu, Isaki, ndi Yakobe.’ Mose adayamba kunjenjemera mwakuti sadalimbenso mtima kuti nkupenyako. Apo Chauta adamuuza kuti, ‘Vula nsapato zakozo, chifukwa malo ukupondawo ngopatulika. Ndaona ndithu kuvutika kwa anthu anga amene ali ku Ejipito. Ndamva kudandaula kwao, ndipo ndabwera kudzaŵapulumutsa. Tiye tsopano, ndikutume ku Ejipito.’ “Moseyo ndi yemwe uja amene Aisraele aja adaamkana nkumanena kuti, ‘Adakuika ndani kuti ukhale mkulu wathu ndi muweruzi wathu?’ Yemweyo Mulungu adamtuma kuti akhale mkulu ndi momboli kudzera mwa mngelo uja amene adaamuwonekera pa chitsamba. Moseyo ndiye adaŵatsogolera anthuwo naŵatulutsa m'dziko la Ejipito. Ankachita zozizwitsa ndi zizindikiro ku Ejipito, pa Nyanja Yofiira, ndiponso m'chipululu zaka makumi anai. Mose yemweyo ndiye amene adauza Aisraele kuti, ‘Mulungu adzatuma wina kuchokera mwa abale anu kuti akhale Mneneri wanu monga ine.’ Moseyo ndi yemwe uja amene anali nao pa msonkhano wa Aisraele m'chipululu. Iye adaaimirira pakati pa makolo athu ndi mngelo uja amene adalankhula naye ku phiri la Sinai. Ndiye amene adalandira mau opatsa moyo kuti adzatininkhe ife. “Koma makolo athu aja adakana kumumvera, m'malo mwake adamkankhira kumbali. Mitima yao idatembenukira za ku Ejipito. Choncho adauza Aroni kuti, ‘Tipangireni milungu kuti izititsogolera, pakuti sitikudziŵa chimene chamgwera Mose uja, amene adatitsogolera potuluka m'dziko la Ejipito.’ Tsono masiku amenewo iwo adapanga fano la mwanawang'ombe. Adapereka nsembe kwa fanoli, nakondwerera ntchito za manja ao. Pamenepo Mulungu adaŵafulatira, naŵapereka ku machimo akupembedza nyenyezi, monga akunenera mau olembedwa m'buku la aneneri kuti, “ ‘Inu Aisraele, musayese kuti munkapereka kwa Ine nyama zimene munkapha ndi kuzipereka ngati nsembe pa zaka makumi anai zija m'chipululu. Munkanyamula hema la Moleki, ndi nyenyezi ya mulungu wanu Refani, mafano amene mudaŵapanga kuti muziŵapembedza. Ndidzakuchotsani kukutayani kutali, kupitirira dziko la Babele.’ “Makolo athu anali ndi chihema cha umboni m'chipululu muja. Adachipanga monga momwe Mulungu adaauzira Mose ndiponso molingana ndi chithunzi chimene Mose adaachiwona. Chihemacho chimene makolo athu adachilandira kwa makolo ao aja, adabwera nacho kuno Yoswa akuŵatsogolera pamene adalanda dziko kwa mitundu ya anthu imene Mulungu adaipitikitsa iwo akufika. Chidakhala pakati pao mpaka nthaŵi ya Davide. Davideyo, Mulungu adamkomera mtima, ndipo adapempha Mulunguyo kuti amlole kumangira nyumba Iye amene ali Mulungu wa Yakobe. Koma Solomoni ndiye adammangira nyumbayo. Ngakhale zinali choncho Mulungu Wopambanazonse sakhala m'nyumba zomangidwa ndi manja, monga akunenera mneneri kuti, “Chauta akuti, ‘Kumwamba ndi mpando wanga waufumu, dziko lapansi ndi chopondapo mapazi anga. Kodi mudzandimangira nyumba yotani? Kapena malo opumuliramo Inewo ngotani? Kodi si manja anga omwe amene adapanga zonsezi?’ ” Stefano adapitirira nati, “Ha, anthu okanika inu, mitima yanu njachikunja, makutu anu ngogontha. Nthaŵi zonse, monga ankachitira makolo anu, inunso mumakana kumvera Mzimu Woyera. Kodi alipo mneneri ndi mmodzi yemwe amene makolo anu aja sadamzunze? Iyai, iwo adapha anthu amene ankaneneratu za kudza kwake kwa Wolungama uja. Tsopano inuyo mudampereka kwa adani ake ndi kumupha. Inu mudaalandira Malamulo a Mulungu kudzera mwa angelo, komabe simudaŵasunge konse.” Pamene abwalo aja adamva mau a Stefanowo, adakwiya kwabasi, namchitira tsinya. Koma Stefano, atadzazidwa ndi Mzimu Woyera, adayang'ana kumwamba naona ulemerero wa Mulungu, ndiponso Yesu ataimirira ku dzanja lamanja la Mulungu. Tsono adati, “Onani! Ndikuwona Kumwamba kotsekuka, ndipo Mwana wa Munthu ataimirira ku dzanja lamanja la Mulungu.” Koma iwo adafuula kwambiri, natseka m'makutu mwao, namgudukira onse pamodzi. Adamtulutsira kunja kwa mzinda, nakamponya miyala. Mboni zidasungiza zovala zao munthu wachinyamata wina, dzina lake Saulo. Pamene anthuwo ankamuponya miyala, Stefano adayamba kupemphera kuti, “Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.” Ndipo adagwada pansi nafuula kwakukulu kuti, “Ambuye, musaŵaŵerengere tchimoli.” Atanena mau ameneŵa, adafa. Saulo uja ankavomerezana nawo za kupha kumeneku. Tsiku limenelo mpingo wa ku Yerusalemu udayamba kuzunzidwa kwambiri, ndipo onse, kupatula atumwi okha, adabalalikira ku madera onse a Yudeya ndi Samariya. Anthu ena okonda Mulungu adakaika maliro a Stefano namlira kwambiri. Koma Saulo uja ankapasula Mpingo. Ankaloŵa m'nyumba za anthu, namagwira amuna ndi akazi omwe, nkumaŵaponya m'ndende. Okhulupirira amene adabalalika aja adapita m'dziko monse akulalika Uthenga Wabwino. Filipo adatsikira ku mzinda wa ku Samariya, namalalikira anthu akumeneko za Khristu, Mpulumutsi wolonjezedwa uja. Makamu a anthu ndi mtima umodzi ankatchera makutu ku zimene Filipo ankanena. Onse ankamvetsera mau ake nkumaona zozizwitsa zimene iye ankachita. Pakuti mizimu yonyansa inkatuluka mwa anthu ambiri amene anali atagwidwa nayo, nimafuula kwambiri. Ndipo ambiri amene anali akufa ziwalo kapena opunduka, ankachira. Choncho munali chimwemwe chachikulu mumzinda muja. Koma mumzindamo munali munthu wina, dzina lake Simoni amene kale ankachita matsenga, namadodometsa anthu onse a ku Samariyako. Iyeyu ankadzimveketsa kuti ndi munthu wamkulu. Anthu onse, aang'ono ndi aakulu omwe, ankamumvera namamtsata nkumanena kuti, “Munthu ameneyu ndiye mphamvu ya Mulungu ija amati, Mphamvu yaikulu.” Ankamutsata chifukwa pa nthaŵi yaitali ankaŵadodometsa ndi matsenga akewo. Koma pamene Filipo ankalalika Uthenga Wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu, ndiponso za dzina la Yesu Khristu, anthu adakhulupirira, ndipo adabatizidwa, amuna ndi akazi omwe. Simoni uja nayenso adakhulupirira, ndipo atabatizidwa, ankakhalira limodzi ndi Filipo. Adazizwa pakuwona zizindikiro ndi zozizwitsa zimene zinkachitika. Pamene atumwi okhala ku Yerusalemu adamva kuti anthu a ku Samariya alandira mau a Mulungu, adatumako Petro ndi Yohane. Iwowo atafika, adayamba kupempherera okhulupirira aja kuti alandire Mzimu Woyera. Nthaŵiyo nkuti Mzimu Woyera asanafike pa wina aliyense mwa iwo. Onsewo anali atangobatizidwa m'dzina la Ambuye Yesu. Tsono Petro ndi Yohane adaŵasanjika manja, ndipo adalandira Mzimu Woyera. Simoni uja ataona kuti Mzimu Woyera waperekedwa kwa iwo atumwi aja ataŵasanjika manja, adafuna kuŵapatsa ndalama atumwiwo. Adati, “Bwanji mutandipatsako inenso mphamvu imeneyi, kuti aliyense amene ndikamsanjike manja, akalandire Mzimu Woyera.” Petro adamuyankha kuti, “Ndalama zakozo ukatayike nazo pamodzi. Iwe ukuganiza kuti ungathe kupata mphatso ya Mulungu pakupereka ndalama kodi? Ulibe gawo kapena malo pa ntchito imeneyi, pakuti mtima wako suli wolungama pamaso pa Mulungu. Nchifukwa chake tembenuka mtima, uleke choipa chakochi. Pempha Ambuye kuti mwina mwake nkukukhululukira maganizo a mumtima mwakoŵa. Pakuti ndakuwona kuti ndiwe wodzaza ndi ndulu yoŵaŵa, ndiponso ndiwe womangidwa ndi maunyolo a zoipa.” Apo Simoni uja adati, “Mundipempherere inuyo kwa Ambuye kuti zimene mwanenazi zisandigwere.” Petro ndi Yohane atatha kupereka umboni wao ndi kulalika mau a Ambuye, adabwerera ku Yerusalemu. Ankapita nalalika Uthenga Wabwino m'midzi yambiri ya Asamariya. Mngelo wa Ambuye adauza Filipo kuti, “Nyamuka, pita chakumwera, kutsata mseu wopita ku Gaza kuchokera ku Yerusalemu; mseu wodzera m'chipululu uja.” Filipo adanyamukadi napita. Ndipo munthu wina wa ku Etiopiya adaabwera ku Yerusalemu kudzapembedza. Iyeyu anali nduna yaikulu ya m'banja la mfumukazi Kandake wa ku Etiopiya, ndiponso woyang'anira chuma chake chonse. Nthaŵi imeneyo ankabwerera kwao. Anali pa galeta akuŵerenga buku la mneneri Yesaya. Tsono Mzimu Woyera adauza Filipo kuti, “Pita, kayandikane nalo galetalo.” Filipo adathamangira nduna ija, ndipo adaimva ikuŵerenga buku la mneneri Yesaya. Tsono adaifunsa kuti, “Bwana, kodi mukumvetsa zimene mukuŵerengazi?” Iye adati, “Ha, ndingamvetse bwanji popanda wina wondimasulira?” Motero adaitana Filipo kuti adzakwere ndi kukhala naye pagaletapo. Mau a m'Malembo amene ankaŵerengawo ndi aŵa: “Iye anali ngati nkhosa yoitsogoza pokaipha, ngati mwana wankhosa wongokhala duu pomumeta. Sadalankhulepo kanthu. Adampeputsa, pa mlandu wake sadamchitire chilungamo. Palibe amene adzatha kusimba za zidzukulu zake, pakuti moyo wake wachotsedwa pa dziko lapansi.” Pamenepo nduna ija idati, “Pepani, tandiwuzani, kodi zimenezi mneneriyo akunena za yani, za iye mwini, kapena za wina?” Apo Filipo adayamba kumlalikira Uthenga Wabwino wa Yesu kuyambira pa Malembo ameneŵa. Ndipo pamene ankapita mumseumo, adafika pena pamene panali madzi. Nduna ija idati, “Madzi si aŵa. Monga pali choletsa kuti ndisabatizidwe?” [ Filipo adayankha kuti, “Mungathe kubatizidwa ngati mukhulupirira ndi mtima wanu wonse.” Iye adati, “Ndikukhulupirira kuti Yesu Khristu ndi Mwana wa Mulungu.”] Pamenepo ndunayo idalamula kuti galetalo liime. Aŵiri onsewo, Filipo ndi nduna ija, adatsikira ku madzi, Filipo nkumubatiza. Pamene adatuluka m'madzimo, Mzimu wa Ambuye adamchotsapo Filipo uja. Ndipo nduna ija siidamuwonenso, koma idapitirira ulendo wake ikusangalala. Tsono Filipo adapezeka kuti ali ku Azoto. Adapita m'dziko monse akulalika Uthenga Wabwino m'mizinda yonse, mpaka adakafika ku Kesareya. Saulo uja ankaopsezabe ophunzira a Ambuye, nkumafuna kuŵapha. Adapita kwa mkulu wa ansembe onse kukampempha makalata opita nawo ku nyumba zamapemphero za ku Damasiko. Ankafuna kuti ngati akapezeko ena otsata Njira ya Ambuye, kaya ndi amuna kaya ndi akazi, akaŵamange nkubwera nawo ku Yerusalemu. Ali paulendo wakewo, adayandikira mzinda wa Damasiko uja. Mwadzidzidzi kuŵala kochokera kumwamba kudamzinga. Adagwa pansi namva mau akuti, “Saulo, Saulo, ukundizunziranji Ine?” Iye adafunsa kuti, “Ndinu yani, Ambuye?” Iwo adati, “Ndine Yesu amene ukundizunza. Koma dzuka, kaloŵe mumzindamo, ndipo akakuuza chochita.” Anthu amene anali naye pa ulendowo adaima, atangoti chete. Mauwo ankaŵamva, koma osaona munthu. Saulo adadzuka, koma pamene maso ake adaphenyuka, sadathe kupenya kanthu. Tsono anzake aja adamgwira pa dzanja naloŵa naye m'Damasiko. Ndipo adakhala masiku atatu osatha kupenya ndiponso osadya kapena kumwa kanthu. Tsono ku Damasikoko kunali wophunzira wina, dzina lake Ananiya. Iyeyu adaaona m'masomphenya Ambuye akumuitana kuti, “Ananiya!” Iye adati, “Ee, Ambuye.” Apo Ambuye adamuuza kuti, “Nyamuka, upite ku mseu wa mumzindamu umene amati, ‘Njira Yolunjika.’ Ndipo ku nyumba ya Yudasi ukafune munthu wina wa ku Tariso, dzina lake Saulo. Panopa akupemphera, ndipo waona m'masomphenya munthu wina, dzina lake Ananiya, akuloŵa ndi kumsanjika manja kuti apenyenso.” Atamva zimenezo Ananiya adati, “Ambuye, anthu ambiri andiwuza za munthu ameneyu, kuti adaŵachita zoipa zambiri anthu anu ku Yerusalemu. Ndipo wabwera kuno ndi ulamuliro wa akulu a ansembe kuti adzamange onse otama dzina lanu mopemba.” Koma Ambuye adamuuza kuti, “Pita, pakuti iyeyu ndi mtumiki wanga amene ndidamsankha kuti akalalikire dzina langa anthu a mitundu ina, mafumu, ndiponso Aisraele. Ine ndidzamuwonetsa zoŵaŵa zonse zimene adzayenera kumva chifukwa cha Ine.” Pamenepo Ananiya adanyamuka nakaloŵa m'nyumbamo. Adamsanjika manja Sauloyo nati, “Mbale wanga Saulo, Ambuye Yesu amene adakuwonekera pa njira imene wadzera ija, andituma. Akufuna kuti upenyenso, ndipo udzazidwe ndi Mzimu Woyera.” Pompo m'maso mwake mudachoka zinthu zonga mamba a nsomba, ndipo adayambanso kupenya. Adaimirira nabatizidwa, ndipo atadya chakudya, adapezanso mphamvu. Saulo adakhala masiku angapo limodzi ndi ophunzira a ku Damasiko. Ndipo posakhalitsa adayamba kulalika m'nyumba zamapemphero za Ayuda kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu. Anthu onse amene ankamva mau akewo ankadabwa, namafunsana kuti, “Kodi ameneyu si yemwe uja amene ku Yerusalemu ankapha anthu otama dzinali mopemba? Kodi siwabwera kuno kuti aŵamange otereŵa ndi kukaŵapereka kwa akulu a ansembe?” Tsono mphamvu za Saulo zinkakulirakulira, ndipo adathetsa nzeru Ayuda okhala ku Damasiko pakuŵatsimikizira kuti Yesu ndiyedi Mpulumutsi wolonjezedwa uja. Patapita masiku ambiri, Ayuda adapangana kuti aphe Saulo, koma anthu ena adamuuzako za chiwembucho. Anthu achiwembuwo ankadikira pa zipata za linga la mzinda usana ndi usiku kuti amuphe. Koma ophunzira ake adamtenga usiku, namtsitsira kunja kwa lingalo m'dengu. Saulo atafika ku Yerusalemu, adayesa kuloŵa m'gulu la ophunzira aja. Koma onse adachita naye mantha, osakhulupirira kuti nayenso ndi wophunzira. Pamenepo munthu wina, dzina lake Barnabasi, adamtenga napita naye kwa atumwi. Iye adaŵafotokozera za m'mene Saulo adaaonera Ambuye panjira paja, ndipo kuti Ambuye adaalankhula naye. Adaŵasimbiranso za m'mene Saulo ku Damasiko ankalankhulira molimba mtima m'dzina la Yesu. Tsono Saulo adakhala nawo, nayendera Yerusalemu yense akulalika molimba mtima m'dzina la Ambuye. Ankalankhulanso ndi kumatsutsana ndi Ayuda olankhula Chigriki, koma iwowo ankafunafuna kumupha. Pamene abale adamva zimenezi, adapita naye ku Kesareya namtumiza ku Tariso. Pamenepo Mpingo ku Yudeya konse, ku Galileya ndi ku Samariya unali pa mtendere. Udakhazikika, ndipo anthu ochuluka adaloŵamo chifukwa anthu ake ankayenda moopa Ambuye, ndipo Mzimu Woyera ankaŵalimbikitsa. Pamene Petro ankayendera anthu a Mulungu uku ndi uku, adakafika kwa amene ankakhala ku Lida. Kumeneko adapezako munthu wina, dzina lake Eneya, amene anali atagona pa mphasa zaka zisanu ndi zitatu, ali wofa ziwalo. Tsono Petro adamuuza kuti, “Eneya, Yesu Khristu akukuchiritsa. Dzuka, yalula mphasa yako.” Pomwepo iye adadzukadi. Anthu onse okhala ku Lida ndi ku Saroni atamuwona, adatembenukira kwa Ambuye. Ku Yopa kunali wophunzira wina wamkazi, dzina lake Tabita (pa Chigriki amati Dorika). Iyeyu ankachita ntchito zabwino zambiri ndi kumathandiza osauka. Masiku amenewo maiyo adaadwala, nkumwalira. Anthu adatsuka maliro, nakagoneka mtembo m'chipinda cham'mwamba. Ku Yopa kunali kufupi ndi ku Lida, choncho pamene ophunzira adamva kuti Petro ali ku Lida, adatuma anthu aŵiri kuti akamuuze kuti, “Chonde, mubwere kwathu kuno msanga.” Tsono Petro adanyamuka napita nawo. Pamene iye adafika, adamperekeza ku chipinda cham'mwamba chija. Akazi onse amasiye adangoti kwete m'mbali mwakemu, akungolira, nkumamuwonetsa malaya ndi zovala zina zimene Dorika ankasoka ali nawo pamodzi. Petro adaŵapempha onse kuti atuluke, ndipo adagwada pansi nkumapemphera. Kenaka adatembenukira mtembo uja nati, “Tabita, dzuka!” Apo Tabita adatsekula maso, ndipo pamene adaona Petro, adakhala tsonga. Petro adamgwira dzanja namuimiritsa. Ndipo adaitana anthu a Mulungu ndi azimai amasiye aja, nampereka kwa iwo ali wamoyo. Anthu onse a ku Yopa adamva zimenezi, ndipo ambiri adakhulupirira Ambuye. Tsono Petro adakhala ku Yopa masiku ambiri kwa munthu wina, dzina lake Simoni, mmisiri wa zikopa. Ku Kesareya kunali munthu wina, dzina lake Kornelio. Iyeyu anali mkulu wa asilikali 100 achiroma, a m'gulu lotchedwa “Gulu la ku Italiya.” Anali munthu wotsata zachipembedzo, ndipo iye pamodzi ndi banja lake lonse ankaopa Mulungu. Ankathandiza kwambiri Ayuda osauka, ndipo ankapemphera Mulungu nthaŵi ndi nthaŵi. Tsiku lina dzuŵa litapendeka, nthaŵi ili ngati 3 koloko, adaona zinthu m'masomphenya. Adaona bwino ndithu mngelo wa Mulungu akubwera kwa iye nkunena kuti, “Kornelio!” Iye adayang'anitsitsa mngeloyo mantha atamgwira, ndipo adamufunsa kuti, “Nkwabwino, Ambuye?” Mngeloyo adati, “Mulungu wakondwera nawo mapemphero ako ndipo wakumbukira ntchito zako zachifundo zako. Tsopano tuma anthu ku Yopa kuti akaitane munthu wina, dzina lake Simoni, wotchedwanso Petro. Akukhala kwa Simoni wina, mmisiri wa zikopa, amene nyumba yake ili m'mbali mwa nyanja.” Mngelo amene ankalankhula naye uja atachoka, Kornelio adaitana antchito ake aŵiri, ndiponso msilikali. Msilikaliyo anali mmodzi mwa amene ankamutumikira, ndipo anali munthu wopembedza Mulungu. Kornelio uja ataŵafotokozera zonse, adaŵatuma ku Yopa. M'maŵa mwake, iwo aja akali m'njira koma akuyandikira mudziwo, Petro adakwera pa denga kukapemphera, nthaŵi ili ngati 12 koloko masana. Ali pamenepo, adamva njala, namafuna kudya. Koma pamene anthu ankakonza chakudya, iye adachita ngati wakomoka. Adaona kuthambo kutatsekuka, chinthu china chikutsikira pansi chooneka ngati chinsalu chachikulu chomangidwa pa nsonga zake zinai. M'menemo munali nyama zamitundumitundu, ndi zokwaŵa, ndiponso mbalame zamumlengalenga. Tsono Petro adamva mau akuti, “Petro dzuka, ipha udye.” Koma Petro adati, “Iyai, pepani Ambuye, ine sindinadyepo ndi kale lonse chinthu chosayera kapena chonyansa.” Kenaka Petro adamvanso kachiŵiri mau akuti, “Zimene Mulungu waziyeretsa, iwe usati nzosayera.” Zimenezi zidachitika katatu, ndipo pompo chinthu chija chidatengedwa kupitanso kumwamba. Petro adayamba kusinkhasinkha za tanthauzo la zimene adaaziwona m'masomphenya zija. Nthaŵi yomweyo anthu amene Kornelio adaaŵatuma aja, ankafunsa za nyumba ya Simoni, ndipo tsopano adaadzaima pa khomo. Adaitana nkufunsa kuti, “Kodi kuli mlendo kuno, dzina lake Simoni, wotchedwanso Petro?” Pamene Petro ankalingalirabe za zimene adaaziwona m'masomphenya zija, Mzimu Woyera adamuuza kuti, “Iwe, anthu atatu akukufuna. Nyamuka, tsika, upite nawo osakayika, pakuti ndaŵatuma ndine.” Apo Petro adatsika nauza anthu aja kuti, “Amene mukumfunayo ndine. Kodi nkwabwino?” Iwo adati, “Kornelio, mkulu wa gulu la asilikali 100, watituma. Iyeyo ndi munthu wolungama ndi woopa Mulungu, ndipo Ayuda onse amamtama. Mngelo wa Mulungu adamuuza kuti akuitaneni kuti mupite kunyumba kwake akamve mau amene muli nawo.” Pamenepo Petro adaŵaloŵetsa m'nyumba, naŵasamala. M'maŵa mwake adanyamuka napita nawo, ndipo abale ena a ku Yopa adamperekeza. M'maŵa mwake adafika ku Kesareya. Kornelio ankaŵadikira, atasonkhanitsa abale ndi abwenzi ake apamtima. Pamene Petro ankati aziloŵa, Kornelio adadzakumana naye, nadzigwetsa kumapazi kwake, namuŵeramira. Koma Petro adamuimiritsa nati, “Iyai, imirirani, inenso ndine munthu chabe.” Ndipo akulankhula naye, adaloŵa napeza anthu ambiri atasonkhana. Pamenepo Petro adaŵauza kuti, “Inu nomwe mukudziŵa kuti Myuda saloledwa konse kuyanjana ndi munthu wa mtundu wina, ngakhale kuloŵa m'nyumba mwake. Koma Mulungu wandidziŵitsa kuti ndisatchule munthu aliyense kuti ngwosayera kapena wonyansa. Nchifukwa chake ndabwera mosaŵiringula pamene mudandiitana. Tsono ndimati ndidziŵe chimene mwandiitanira.” Kornelio adati, “Dzana ilo, ndinkapemphera m'nyumba mwanga, nthaŵi ngati yomwe ino ya 3 koloko dzuŵa litapendeka. Mwadzidzidzi kutsogolo kwangaku kudaimirira munthu wovala zovala zonyezimira. Adandiwuza kuti, ‘Kornelio, Mulungu wamva pemphero lako, ndipo wakumbukira ntchito zako zachifundo. Tsono tuma anthu ku Yopa akaitane Simoni wotchedwa Petro. Iyeyu akukhala kwa Simoni, mmisiri wa zikopa, nyumba yake ili m'mbali mwa njanja.’ Nchifukwa chake ndidaakutumirani anthu msanga, ndipo mwachita bwino kuti mwabwera. Tsopano tonse tili pano pamaso pa Mulungu kuti timve zonse zimene Ambuye akulamulani kuti munene.” Petro adayamba kulankhula, adati, “Zoonadi ndazindikira tsopano kuti Mulungu alibe tsankho. Amalandira bwino munthu wa mtundu uliwonse womuwopa nkumachita chilungamo. Mukudziŵa kuti adatumizira Aisraele mau ake naŵauza Uthenga Wabwino wa mtendere kudzera mwa Yesu Khristu, amene ali Ambuye a anthu onse. Mukudziŵa zimene zidachitika ku Yudeya konse, kuyambira ku Galileya pambuyo pa nthaŵi imene Yohane ankalalika za ubatizo wake. Mukudziŵa za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu adaamudzoza ndi Mzimu Woyera nampatsa mphamvu. Tsono popeza kuti Mulungu anali naye, adapita ponseponse akuchita ntchito zabwino ndi kuchiritsa onse osautsidwa ndi Satana. Ife ndife mboni za zonse zimene Iye adachita mu Yerusalemu ndi m'dziko lonse la Ayuda. Iwo adamupha pakumpachika pa mtanda. Komabe mkucha wake Mulungu adamuukitsa kwa akufa, nalola kuti aonekere poyera. Sadaonekere kwa anthu onse ai, koma kwa mboni zimene Mulungu adazisankhiratu. Ndiye kuti adaonekera kwa ife, amene tinkadya ndi kumwa naye pamodzi atauka kwa akufa. Ndipo adatilamula kuti tikalalikire anthu onse, ndi kuchita umboni kuti Iyeyo ndiye amene Mulungu adamsankha kukhala Woweruza anthu amoyo ndi akufa omwe. Aneneri onse adamchitira umboni, ndi kunena kuti chifukwa cha dzina lake, Mulungu adzakhululukira machimo a munthu aliyense wokhulupirira Iyeyu.” Petro akulankhulabe, Mzimu Woyera adaŵatsikira anthu onse amene ankamva mauwo. Ndipo okhulupirira achiyuda amene adaaperekeza Petro, adadabwa kuti Mulungu adapereka mphatso ya Mzimu Woyera ndi kwa anthu akunja omwe. Pakuti adaŵamva akulankhula zilankhulo zosadziŵika ndi kutamanda ukulu wa Mulungu. Tsono Petro adati, “Anthu aŵa alandira Mzimu Woyera monga ife. Nanga alipo amene angaŵaletse kubatizidwa ndi madzi?” Motero adalamula kuti abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Ndipo anthuwo adampempha kuti akhale nawo masiku angapo. Atumwi aja, ndiponso abale onse amene anali ku Yudeya, adamva kuti anthu a mitundu ina nawonso alandira mau a Mulungu. Tsono pamene Petro adabwera ku Yerusalemu, a m'gulu lolimbikira za kuumbala adatsutsana naye. Iwo adati, “Inu mudaloŵa m'nyumba ya anthu osaumbalidwa, nkudya nawo pamodzi.” Apo Petro adayamba kuŵafotokozera mwatsatanetsatane zimene zidachitika. Adati, “Ine ndinkapemphera m'mudzi wa Yopa. Ndidaachita ngati kukomoka, ndiye ndidaona ngati kutulo chinthu china chikutsika pansi kuchokera kumwamba. Chinkaoneka ngati chinsalu chachikulu chomangidwa pa nsonga zake zinai, ndipo chidafika pamene panali ineyo. Nditachipenyetsetsa, ndidaonamo nyama zoŵeta ndi zakuthengo ndiponso zokwaŵa ndi mbalame zamumlengalenga. Tsono ndidamva mau ondiwuza kuti, ‘Petro dzuka, ipha, udye.’ Koma ine ndidati, ‘Iyai pepani Ambuye, ine ndi kale lonse chinthu chosayera kapena chonyansa sichinaloŵepo pakamwa pangapa.’ Koma mau ochokera kumwamba aja adanenanso kachiŵiri kuti, ‘Zimene Mulungu waziyeretsa, iwe usati nzosayera.’ Zimenezi zidachitika katatu, ndipo zonsezo zinatengedwa kupitanso kumwamba. Nthaŵi yomweyo kudafika anthu atatu kunyumba kumene ndinkakhala. Adaatumidwa kwa ine kuchokera ku Kesareya. Mzimu Woyera anali atandiwuza kuti ndisakayike konse, koma ndipite nawo. Abale asanu ndi mmodzi aŵa nawonso adandiperekeza, ndipo tidakaloŵa m'nyumba ya Kornelio. Iyeyo adatisimbira za m'mene adaaonera mngelo ataimirira m'nyumba mwake nkumuuza kuti, ‘Tuma anthu ku Yopa kuti akaitane Simoni, wotchedwa Petro. Iyeyo adzakuuza mau amene iwe udzapulumuka nawo, ndiponso onse a m'banja mwako.’ Tsono pamene ndidayamba kulankhula, Mzimu Woyera adaŵatsikira iwowo, monga momwe adaatitsikiranso ife poyamba paja. Pamenepo ndidakumbukira mau aja amene adaalankhula Ambuye akuti, ‘Yohane adabatiza ndi madzi, koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.’ Tsono ngati Mulungu adaŵapatsa iwowo mphatso yomweyo imene adapatsa ifeyo pamene tidakhulupirira Ambuye Yesu Khristu, nanga ine ndine yani kuti ndikadatha kumletsa Mulungu?” Pamene otsutsana naye aja adamva zimenezi, adaleka mitsutsoyo. Adatamanda Mulungu adati, “Kodi kani! Ndiye kuti Mulungu wapatsadi ndi akunja omwe mwai woti atembenuke mtima ndi kulandira moyo!” Okhulupirira Khristu aja, amene anali atabalalikana chifukwa cha mazunzo omwe adabuka pa nkhani ija ya Stefano, adafika mpaka ku Fenisiya, ku Kipro, ndiponso ku Antiokeya. Sankalalika mau kwa munthu wina aliyense, koma kwa Ayuda okha. Koma pakati pao panali ena ochokera ku Kipro ndiponso ku Kirene. Ameneŵa adafika ku Antiokeya nayamba kulankhulanso ndi Agriki nkumaŵalalikira Uthenga Wabwino wonena za Ambuye Yesu. Ambuye ankaŵalimbikitsa, mwakuti anthu ambiri adakhulupirira natembenukira kwa Ambuye. Mpingo wa ku Yerusalemu utamva zimene zidachitikazo, udatuma Barnabasi ku Antiokeyako. Pamene iye adafika kumeneko nkuwona m'mene Mulungu adaŵadalitsira, adakondwa, nalimbikitsa onsewo kuti atsimikize mtima kukhala okhulupirika kwa Ambuye. Barnabasiyo anali munthu wolungama, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera ndi chikhulupiriro. Choncho anthu ambirimbiri adakopeka nadzipereka kwa Ambuye. Pamenepo Barnabasi adapita ku Tariso kukafuna Saulo. Atampeza, adabwera naye ku Antiokeya. Iwo adakhala pamodzi mu mpingo umenewo chaka chathunthu, naphunzitsa anthu ambirimbiri. Ndi ku Antiokeya kumene ophunzira adayamba kutchedwa Akhristu. Masiku amenewo kudafika aneneri ena ku Antiokeya ochokera ku Yerusalemu. Mmodzi mwa iwo, dzina lake Agabu, adaimirira, ndipo ndi mphamvu za Mzimu Woyera adalosa kuti padzakhala njala yaikulu pa dziko lonse lapansi. Njalayo idabweradi pa nthaŵi ya Klaudio. Pamenepo Akhristu aja adatsimikiza zotumiza thandizo kwa abale okhala ku Yudeya, ndipo kuti aliyense atumize molingana ndi kupata kwake. Zimenezi adachitadi, ndipo anatuma Barnabasi ndi Saulo kukapereka thandizolo kwa akulu a mpingo. Pafupi ngati nthaŵi imeneyo mfumu Herode adagwira ena a mu Mpingo kuti aŵazunze. Adalamula kuti Yakobe, mbale wake wa Yohane, aphedwe ndi lupanga. Ndipo ataona kuti zimenezi zidakondweretsa Ayuda, adapitiriza ndithu nkugwiranso Petro. Zimenezi zidachitika pa masiku a Paska, chikondwerero cha mikate yosafufumitsa. Atamgwira, adamtsekera m'ndende, nampereka kwa magulu anai a asilikali kuti azimlonda, gulu lililonse asilikali anai. Tsono Herode ankafuna kuzenga mlandu wake pamaso pa anthu onse, chikondwerero cha Paska chitapita. Motero Petro ankasungidwa m'ndende. Koma Mpingo unkamupempherera kwa Mulungu kosalekeza. Usiku woti m'maŵa mwake Herode azenga mlandu wake, Petro adaagona pakati pa asilikali aŵiri. Anali womangidwa ndi maunyolo aŵiri, ndipo pakhomo pa ndende panali alonda ena. Mwadzidzidzi kudafika mngelo wa Ambuye ndipo kuŵala koti mbee kudaunika m'chipindamo. Mngeloyo adagunduza Petro m'nthitimu kuti amdzutse, ndipo adati, “Dzuka msanga!” Pompo maunyolo aja adakolopoka m'manja mwake. Kenaka mngelo uja adamuuza kuti, “Vala lamba wako ndi nsapato zako.” Petro atachita zimenezi mngelo uja adamuuzanso kuti, “Fundira mwinjiro wako, unditsate.” Apo Petro adatuluka namtsata, osazindikira kuti zimene mngelo ankachitazo nzoona. Ankangoyesa kuti akuwona zinthu m'masomphenya chabe. Onsewo adapitirira gulu loyamba la asilikali aja, kenaka lachiŵiri, mpaka kukafika pa chitseko chachitsulo cha pa chipata choloŵera mu mzinda. Chitsekocho chidangodzitsekukira chokha, iwowo nkutuluka. Adayenda ndithu mu mseu wina wamumzindamo. Atafika polekezera pake mngelo uja adamchokera. Pamenepo Petro adadzidzimuka nati, “Tsopano ndikudziŵadi kuti Ambuye anatuma mngelo wao ndipo andipulumutsa kwa Herode, ndi ku zoipa zonse zimene Ayuda ankayembekeza kuti zidzandichitikira.” Atazindikira zimenezi, adapita kunyumba kwa Maria, amai ake a Yohane wotchedwanso Marko. Anthu ambiri anali atasonkhana kumeneko akupemphera. Pamene Petro adagogoda pa chitseko chapakhomo, mtsikana wina, dzina lake Roda, adabwera kuti amtsekulire. Atazindikira liwu lake kuti ndi la Petro, adakondwa kwambiri, kotero kuti sadatsekule chitsekocho, koma adathamangiranso m'kati nakawuza ena aja kuti, “Petro ali pakhomopa!” Anthuwo adati, “Wapenga iwe!” Koma iye adalimbikira kuti nzoonadi. Apo iwo adati, “Ndi mngelo wake ameneyo.” Koma Petro ankangogogodabe. Pamene adamtsekulira nkuwona kuti ndiyedi, adangoti kakasi. Petro adakweza dzanja kuti iwo akhale chete, naŵafotokozera m'mene Ambuye adaamtulutsira m'ndende muja. Ndipo adati, “Mumuuze Yakobe ndi abale ena aja zimenezi.” Pamenepo iye adatuluka napita kwina. Kutacha, asilikali aja adasokonezeka kwabasi nati, “Petro wapita kuti?” Herode adamufunafuna, koma osampeza. Adaŵazenga mlandu alonda aja, nalamula kuti aphedwe. Pambuyo pake Herode adachoka ku Yudeya kupita ku Kesareya, nakakhala kumeneko. Herode adaaŵakwiyira anthu a ku Tiro ndi a ku Sidoni. Tsono anthuwo adadza pamodzi kwa iye. Adaayamba akopa Blasito, kapitao wa ku nyumba ya mfumu kenaka nkukapempha mtendere, chifukwa chakudya cha m'dziko laolo chinkachokera m'dziko la mfumuyo. Adapangana tsiku, ndipo pa tsikulo Herode adavala zovala zake zachifumu nkukhala pa mpando wake wachifumu, nayamba kuŵalankhula anthu aja. Anthuwo adanena mokweza mau kuti, “Ameneŵa ndi mau a mulungu, osati a munthu ai.” Pompo mngelo wa Ambuye, adamkantha Herodeyo chifukwa sadapereke ulemu kwa Mulungu. Mphutsi zidamudya ndipo adafa. Koma mau a Mulungu adanka nafalikirafalikira. Tsono Barnabasi ndi Saulo atakwaniritsa zimene adaaŵatumira ku Yerusalemu, adabwerako. Adatengako Yohane wotchedwa Marko uja. Mu mpingo wa ku Antiokeya munali alaliki ndi aphunzitsi aŵa: Barnabasi, Simeoni (wotchedwa Wakuda), Lusio wa ku Kirene, Manaene (amene adaaleredwa pamodzi ndi bwanamkubwa Herode), ndiponso Saulo. Tsiku lina pamene iwo adasonkhana kuti apembedze Ambuye ndi kuti asale zakudya, Mzimu Woyera adaŵauza kuti, “Mundipatulire Barnabasi ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndaŵaitanira.” Tsono atasala zakudya ndi kupemphera adaŵasanjika manja naŵatuma. Barnabasi ndi Saulo, otumidwa ndi Mzimu Woyera aja, adapita ku Seleukiya. Kuchokera kumeneko adayenda m'chombo nakafika ku chilumba cha Kipro. Atafika ku mzinda wa Salami, adalalika mau a Mulungu m'nyumba zamapemphero za Ayuda. Analinso ndi Yohane womaŵathandiza. Iwo adabzola chilumba chonse mpaka kukafika ku mzinda wa Pafosi. Kumeneko adapezako munthu wina wamasenga, dzina lake Barayesu, Myuda amene ankadziyesa mneneri. Iyeyu ankakhala kwa bwanamkubwa Sergio Paulo, munthu wanzeru. Sergio Pauloyo adaitana Barnabasi ndi Saulo, chifukwa iye ankafunitsitsa kumva mau a Mulungu. Koma kumeneko adapezanako ndi Elimasi, wamasenga uja (Elimasi ndiye kuti Wamasenga). Iyeyo adatengana nawo, kuwopa kuti bwanamkubwa uja angakhulupirire. Koma Saulo, amene ankatchedwanso Paulo, atadzazidwa ndi Mzimu Woyera, adampenyetsetsa nati, “Iwe mwana wa Satana, mdani wa chilungamo, wa mtima wa kunyenga kulikonse ndi kuchenjeretsa kwamtundumtundu, udzaleka liti kupotoza njira zolungama za Ambuye? Ona dzanja la Ambuye likukantha tsopano apa. Ukhala wakhungu osaonanso dzuŵa pa kanthaŵi.” Nthaŵi yomweyo khungu ndi mdima zidamgweradi, ndipo adayamba kufunafuna anthu oti amgwire dzanja ndi kumtsogolera. Pamene bwanamkubwa uja adaona zimene zidachitikazo, adakhulupirira. Adaadabwa nazo zimene iwo adaaphunzitsa za Ambuye. Paulo ndi anzake adayenda m'chombo kuchokera ku Pafosi kukafika ku Perga m'dera la Pamfiliya. Koma Yohane adaŵasiya nabwerera ku Yerusalemu. Kuchokera ku Perga iwo adapitirira nakafika ku Antiokeya m'dera la Pisidiya. Pa tsiku la Sabata adaloŵa m'nyumba yamapempherero ya Ayuda, nakhala pansi. Ataŵerengedwa mau a m'buku la Malamulo a Mose ndi m'buku la aneneri, akulu a nyumba yamapemphero ija adaŵatumira mau oŵauza kuti, “Abale, ngati muli ndi mau olimbikitsa nawo anthuŵa, nenani.” Apo Paulo adaimirira nakweza dzanja kuti anthu akhale chete, ndipo adayamba kulankhula. Adati, “Inu Aisraele, ndi ena nonse oopa Mulungu, mverani. Mulungu wa mtundu wathu wa Aisraele, adasankha makolo athu, ndipo adaŵakuza pamene anali alendo ku dziko la Ejipito. Adaŵatulutsa m'dzikomo ndi dzanja lake lamphamvu, adaŵasamalabe mopirira m'chipululu zaka makumi anai. Iye adaononga mitundu isanu ndi iŵiri ya anthu m'dziko la Kanani, napereka dziko lao kwa Aisraele kuti likhale laolao. Zonsezi zidatenga zaka ngati 450. “Pambuyo pake adaŵapatsa oweruza kufikira nthaŵi ya mneneri Samuele. Kenaka anthu adapempha kuti aŵapatse mfumu, ndipo Mulungu adaŵapatsa Saulo, mwana wa Kisi, munthu wa fuko la Benjamini, iye nkuŵalamulira pa zaka makumi anai. Pambuyo pake Mulungu adamchotsa Sauloyo, naika Davide kuti akhale mfumu yao. Za iyeyu Mulungu adanena kuti, ‘Ndapeza Davide, mwana wa Yese, ndiye munthu wanga wapamtima, amene adzachita zonse zimene Ine ndifuna.’ Mwa zidzukulu za Davideyo Mulungu adasankha Yesu kuti akhale Mpulumutsi wa Aisraele, monga momwe adaalonjezera kale. Iyeyo asanayambe ntchito, Yohane ankalalikira Aisraele onse kuti atembenuke mtima ndi kubatizidwa. Pamene Yohane anali pafupi kutsiriza ntchito yake, adafunsa anthu kuti, ‘Kodi inu mumayesa kuti ine ndine yani? Inetu sindine amene mukumuyembekezayo ai. Koma pakubwera wina pambuyo panga amene ine sindili woyenera ngakhale kumvula nsapato zake.’ “Ine abale, zidzukulu za Abrahamu, ndi ena nonse oopa Mulungu, uthenga wa chipulumutsowu Mulungu watumizira ife. Anthu okhala ku Yerusalemu ndi akulu ao sadamzindikire Yesu, ndipo sadamvetse mau a aneneri amene amaŵerengedwa tsiku la Sabata lililonse. Komabe pakumzenga mlandu Yesuyo kuti aphedwe, adachitadi zimene aneneri adaaneneratu. Ngakhale sadapeze konse chifukwa chomuphera, komabe adapempha Pilato kuti Yesuyo aphedwe. Ndipo atachita zonse zimene zidalembedwa za Iye, adamtsitsapo pa mtanda paja namuika m'manda. Koma Mulungu adamuukitsa kwa akufa, ndipo pa masiku ambiri adakhala akuwonekera kwa anthu aja amene adaamperekeza ku Yerusalemu kuchokera ku Galileya. Amenewo ndiwo amene akumchitira umboni kwa anthu tsopano. Ndipo ife tikukulalikirani Uthenga Wabwino wakuti zilipo zimene Mulungu adaaŵalonjeza makolo athu. Tsono zimene adaalonjezazo Iye watichitire ifeyo, zidzukulu zao, pakuukitsa Yesu kwa akufa. Monganso mudalembedwera m'Salimo lachiŵiri kuti, “ ‘Iwe ndiwe Mwana wanga, Ine lero ndakubala.’ Ndipo zakuti adamuukitsa kwa akufa kuti asaole konse, Mulungu adati, ‘Ndidzakupatsani madalitso opatulika ndi okhulupirika amene ndidalonjeza Davide.’ Nchifukwa chake m'Salimo lina akutinso, “ ‘Simudzalekerera Woyera wanu kuti aole.’ Paja Davide adati atakwaniritsa zimene Mulungu adaakonzeratu pa masiku a mbadwo wake, adamwalira naikidwa m'manda pamodzi ndi makolo ake, ndipo thupi lake lidaola. Koma uja Mulungu adamuukitsa kwa akufayu sadaole ai. Tsono abale, dziŵani kuti chifukwa cha Yesuyo tikukulalikirani zakuti machimo amakhululukidwa. Ndipo kudzera mwa Iye yemweyo aliyense wokhulupirira amapeza chipulumutso chathunthu chimene simukadatha kuchipata potsata malamulo a Mose. Ndiye inu chenjerani kuti zingakugwereni zimene aneneri aja adanena kuti, “ ‘Mvetsani inu anthu onyoza, zizwani ndipo muwonongeke, pakuti pa nthaŵi ya moyo wanu Ine ndidzachita chinthu chimene simungakhulupirire konse, ngakhale wina akuuzeni.’ ” Pamene ankatuluka, anthu aja adapempha Paulo ndi Barnabasi kuti adzaŵakambirenso zomwezi tsiku la Sabata linalo. Anthu osonkhana aja atamwazikana, Ayuda ambiri, ndiponso anthu a mitundu ina otembenuka nkumatsata zachiyuda, adatsatira Paulo ndi Barnabasi. Aŵiriŵa adalankhula ndi anthu aja, naŵapempha kuti alimbikire kutsata zimene Mulungu adaŵachitira mwa kukoma mtima kwake. Pa tsiku la Sabata linalo pafupi anthu onse amumzindamo adasonkhana kuti amve mau a Ambuye. Pamene Ayuda aja adaona anthu ambiriwo, adachita nsanje kwambiri. Adayamba kutsutsa zimene Paulo ankanena, ndipo adamchita chipongwe. Koma Paulo ndi Barnabasi adalankhula molimbika, adati, “Kudaayenera ndithu kuti tiyambe talalika mau a Mulungu kwa inu. Tsono popeza kuti mwaŵakana, ndipo potero mwaonetsa nokha kuti ndinu osayenera kulandira moyo wosatha, ife tikusiyani, tipita kwa anthu akunja. Paja Ambuye adatilamula kuti, “ ‘Ndakuika kuti uunikire anthu akunja, kuti mwa iwe ndipulumutse dziko lonse lapansi.’ ” Pamene anthu a mitundu ina aja adamva zimenezi, adakondwa, nayamikira wawu a Ambuye. Ndipo onse amene Mulungu adaaŵasankha kuti alandira moyo wosatha, adakhulupirira. Mau a Ambuye adafalikira m'dziko monse muja. Koma Ayuda aja adautsa mitima ya akazi ena apamwamba opembedza Mulungu, ndiponso ya atsogoleri achimuna amumzindamo. Tsono adayambitsa mazunzo osautsa Paulo ndi Barnabasi, naŵapirikitsa m'dziko mwaomo. Koma iwo adasansa fumbi la kumapazi kwao moŵatsutsa, napita ku Ikonio. Ndipo ophunzira a ku Antiokeya adadzazidwa ndi Mzimu Woyera ndipo adakhala ndi chimwemwe chachikulu. Zimene zidachitika ku Antiokeya, zidachitikanso ku Ikonio. Paulo ndi Barnabasi adaloŵa m'nyumba yamapemphero ya Ayuda. Adaphunzitsa mwamphamvu, kotero kuti anthu ambirimbiri, Ayuda ndiponso anthu a mitundu ina, adakhulupirira. Koma Ayuda amene sadakhulupirire adautsa mitima ya akunjawo kuti adane ndi akhristu. Paulo ndi Barnabasi adakhala komweko kanthaŵi ndithu, akulalika molimba mtima za kukoma mtima kwa Ambuye. Ndipo Ambuye ankachitira umboni mau ao pakuŵapatsa mphamvu zochitira zizindikiro ndi zozizwitsa. Koma anthu amumzindamo adagaŵikana, ena anali mbali ya Ayuda, ena anali mbali ya atumwi. Pamenepo anthu akunja ndi Ayuda, pamodzi ndi akulu ao, adatsimikiza zoŵazunza ndi kuŵaponya miyala. Atumwi aja atamva zimenezi, adathaŵira ku Listara ndi ku Deribe, mizinda ya ku Likaoniya, ndiponso ku dziko lozungulira mizindayo. Kumenekonso adayamba kulalika Uthenga Wabwino. Ku Listara kunali munthu wina wopunduka miyendo amene ankangokhala pansi. Adaabadwa wolumala ndipo chikhalire chake sadayende. Iyeyo ankamvetsera pamene Paulo ankalankhula. Paulo adampenyetsetsa, ndipo ataona kuti munthuyo ali ndi chikhulupiriro choti nkuchira, adanena mokweza mau kuti, “Wongola miyendo yako, imirira.” Pomwepo munthuyo adadzambatuka nkuyamba kuyenda. Pamene anthu onse aja adaona zimene Paulo adachita, adafuula m'Chilikaoniya kuti, “Yatitsikira milungu yooneka ngati anthu.” Motero Barnabasi adamutcha Zeusi ndipo Paulo adamutcha Heremesi, chifukwa ndiye ankatsogola polankhula. Nyumba yopembedzeramo Zeusiyo inali kunja pafupi ndi mzindawo. Tsono wansembe wake adabwera ku zipata atatenga ng'ombe yozekedwa maluŵa m'khosi. Iyeyo pamodzi ndi anthu onse aja adaafuna kudzapereka nsembe. Koma pamene atumwi aja, Barnabasi ndi Paulo, adamva zimenezi, adang'amba zovala zao, nathamangira pakati pa anthuwo. Adalankhula mokweza mau kuti, “Anthuni, bwanji mukuchita zimenezi? Ifenso ndife anthu monga inu nomwe. Tikukulalikirani Uthenga Wabwino wakuti musiye zinthu zachabezi ndi kutsata Mulungu wamoyo amene adalenga thambo, dziko lapansi, nyanja ndi zonse zili m'menemo. Kale Iye adaalekerera anthu a mitundu yonse kuti azitsata njira zaozao. Komabe sankaleka kudzichitira umboni mwa zabwino zimene amachita. Kuchokera kumwamba amakupatsani mvula ndi nyengo za zipatso. Amakupatsani zakudya ndi zina zambiri zodzaza mitima yanu ndi chimwemwe.” Ngakhale ndi mau ameneŵa, adavutika kuŵaletsa anthu aja kuti asaŵaphere nsembe. Koma kudabwera Ayuda ena ochokera ku Antiokeya ndi ku Ikonio nakopa anthu aja. Tsono anthuwo adamponya Pauloyo miyala, kenaka nkumuguzira kunja kwa mzinda, chifukwa ankayesa kuti wafa. Koma ophunzira ena atasonkhana nkumzungulira, iye adauka naloŵanso mumzindamo. M'maŵa mwake iye ndi Barnabasi adapita ku Deribe. Paulo ndi Barnabasi atalalika Uthenga Wabwino ku Deribe kuja, ndi kukopa okhulupirira ambiri, adabwerera ku Listara, ku Ikonio ndi ku Antiokeya m'dera la Pisidiya. Adaŵalimbitsa mtima ophunzira aja, naŵauzitsa kuti asataye chikhulupiriro chao. Adaŵauza kuti, “Kuti tiloŵe mu Ufumu wa Mulungu tiyenera kupirira masautso ambiri.” Pa mpingo uliwonse adakhazika akulu a mpingo. Ndipo pakupemphera ndi kusala zakudya adaŵapereka kwa Ambuye amene anali atamkhulupirira tsopano. Pambuyo pake adabzola Pisidiya nakafika ku Pamfiliya. Ndipo atalalika mau a Mulungu ku Perga, adapita ku Ataliya. Kumeneko adaloŵa m'chombo kupita ku Antiokeya kuja, kumene adaaperekedwa kwa Mulungu kuti aŵadalitse pa ntchito imene tsopano anali ataitsiriza. Pamene adafika kumeneko, adasonkhanitsa mpingo wonse, naufotokozera zonse zimene Mulungu adaachita mwa iwo, ndiponso m'mene Iye adaatsekulira anthu a mitundu ina njira kuti akhulupirire. Tsono adakhala komweko ndi ophunzira aja nthaŵi yaitali. Anthu ena ochokera ku Yudeya adabwera ku Antiokeya, namaphunzitsa abale kuti, “Ngati simuumbala potsata mwambo wa Mose, simungathe kupulumuka.” Koma Paulo ndi Barnabasi adatsutsana nawo kolimba. Tsono abale adapangana kuti Paulo ndi Barnabasi, ndi abale ena a ku Antiokeya, apite ku Yerusalemu kukakambirana ndi atumwi ndi akulu a mpingo za nkhaniyi. Mpingo utaŵatuma, adadzera ku Fenisiya ndi Samariya akufotokoza za m'mene anthu osakhala Ayuda adatembenukira mtima. Mau ameneŵa adakondweretsa abale onse kwambiri. Pamene adafika ku Yerusalemu, adalandiridwa ndi mpingo ndi atumwi ndi akulu a mpingo. Paulo ndi Barnabasi adaŵafotokozera ntchito zonse zimene Mulungu adaachita mwa iwo. Koma okhulupirira ena amene kale anali a m'gulu la Afarisi, adaimirira nati, “Nkofunika kuti okhulupirira a mitundu ina aumbalidwe, ndiponso aŵalamule kuti azitsata Malamulo a Mose.” Tsono atumwi ndi akulu a mpingo adasonkhana kuti aiwone bwino nkhaniyi. Atakambirana nthaŵi yaitali, Petro adaimirira naŵauza kuti, “Abale anga, mukudziŵa kuti pa masiku oyamba aja Mulungu adandisankha ine pakati pa inu kuti ndilalike Uthenga Wabwino kwa anthu a mitundu ina, kuti amve ndi kukhulupirira. Ndipo Mulungu amene amadziŵa mitima ya anthu, adaŵachitira umboni pakuŵapatsa Mzimu Woyera, monga adapatsira ifeyo. Mulungu sadasiyanitse konse pakati pa ife ndi iwo, koma adayetsera mitima yao ndi chikhulupiriro chao. Tsono mukumuyeseranji Mulungu pakuika m'khosi mwa ophunzirawo goli limene ngakhale makolo athu kapena ife tomwe tidalephera kulisenza? Iyai, timakhulupirira kuti chopulumutsa iwowo, ndi ife tomwe, ndi kukoma mtima kwa Ambuye Yesu.” Onse mumsonkhanomo adangoti chete nkumamvetsera Barnabasi ndi Paulo akufotokoza za m'mene Mulungu adachitira zizindikiro ndi zozizwitsa pakati pa akunja kudzera mwa iwowo. Pamene iwo aja adatha kulankhula, Yakobe adati, “Abale anga, mundimvere. Simoni wafotokoza za m'mene Mulungu pachiyambi pomwe adakumbukira anthu a mitundu ina, pa kupatula ena pakati pao kuti akhale anthu akeake. Zimenezi zikuvomerezana ndi mau a aneneri. Paja kudalembedwa kuti, “ ‘Zitatha zimenezi ndidzabwerera, ndidzamanganso nyumba ya Davide imene idagwa. Ndidzamanganso zopasuka zake, ndi kuikonzanso. Ndidzachita choncho kuti anthu ena onse afunefune Ambuye, ndiye kuti, anthu a mitundu yonse amene amadziŵika ndi dzina langa. Akutero ndi Chauta amene adaulula zimenezi kuyambira kalekale.’ “Nchifukwa chake ine ndikuti, tisaŵavute anthu a mitundu ina amene akutembenuka mtima nkumatsata Mulungu. Koma tiŵalembere kalata kuŵauza kuti asamadye zimene zili zosayera chifukwa zidaperekedwa kwa mafano. Alewe dama, ndipo asamadye nyama zochita kupotola, alewenso magazi. Paja kuyambira kalekale mu mzinda uliwonse muli anthu ophunzitsa Malamulo a Mose, ndipo amaŵerenga mau ake m'nyumba zamapemphero pa tsiku la Sabata lililonse.” Pamenepo atumwi ndi akulu a mpingo, pamodzi ndi mpingo wonse, adavomerezana kusankha anthu ena pakati pao kuti aŵatume ku Antiokeya pamodzi ndi Paulo ndi Barnabasi. Adasankha Yudasi, wotchedwa Barsabasi, ndiponso Silasi, anthu aulemu pakati pa abale, kuti akapereke kalata yonena kuti, “Abale, ife atumwi pamodzi ndi akulu a mpingo tikuti moni inu abale a ku Antiokeya, a ku Siriya, ndi a ku Silisiya, amene simuli Ayuda. Tamva kuti anthu ena ochokera m'gulu lathu akhala akukuvutani ndi kukusokonezani maganizo. Amenewo sitidaŵatume ndife ai. Tsono titasonkhana, tavomerezana kusankha anthu ndi kuŵatuma kwa inu. Adzabwera pamodzi ndi okondedwa athu Barnabasi ndi Paulo. Amene adadzipereka kuti atumikire Ambuye athu Yesu Khristu. Nchifukwa chake tatuma Yudasi ndi Silasi kuti adzakufotokozereni pakamwa zimene talemba m'kalatayi. Maganizo athu agwirizana ndi a Mzimu Woyera kuti tisakusenzetseni katundu wina, kupatula zofunika zokhazi: musamadye chakudya chimene chidaperekedwa nsembe kwa mafano, musamadye magazi kapena nyama yochita kupotola, ndiponso musachite dama. Mukalewa zimenezi, mudzachita bwino. Tsalani bwino.” Tsono otumidwa aja adanyamuka nakafika ku Antiokeya. Adasonkhanitsa mpingo wonse napereka kalata ija. Pamene iwo adaiŵerenga, adakondwa chifukwa cha mau ake oŵalimbikitsa. Yudasi ndi Silasi analinso alaliki, ndipo adalimbikitsa abale aja ndi mau ambiri naŵakhazikitsa mtima. Atakhala kumeneko nthaŵi ndithu, abale aja adaŵalola mwamtendere kuti abwerere kwa amene adaaŵatuma. [ Koma Silasi adatsimikiza kuti akhalire.] Paulo ndi Barnabasi adakhalabe ku Antiokeya, akuphunzitsa ndi kulalika mau a Ambuye pamodzi ndi anthu ena ambiri. Patapita masiku angapo, Paulo adauza Barnabasi kuti, “Tiyeni tibwerere tizinka tiyendera abale ku mzinda uliwonse kumene tidalalikako mau a Ambuye.” Barnabasi adafuna kutenganso Yohane wotchedwa Marko, kuti apite nao. Koma Paulo adaganiza kuti sibwino kumtenganso, chifukwa paja iye adaaŵasiya ku Pamfiliya, osapita nao ku ntchito. Pamenepo iwo adakangana kwambiri, kotero kuti adapatukana. Barnabasi adamtenga Marko uja naloŵa m'chombo kupita ku Kipro. Koma Paulo adasankhula Silasi, ndipo abale ataŵapempherera kuti Ambuye aŵadalitse, adanyamuka. Adadzera ku Siriya ndi ku Silisiya akulimbikitsa anthu amumpingo. Paulo adafika ku Deribe ndi ku Listara. Kumeneko kunali wophunzira wina, dzina lake Timoteo. Mai wake anali Myuda wosanduka wokhulupirira, koma bambo wake anali Mgriki. Abale a ku Listara ndi a ku Ikonio ankamtama Timoteoyo. Motero Paulo adafuna kuti iye amperekeze. Tsono adamuumbala chifukwa cha Ayuda amene anali kumeneko, pakuti onse ankadziŵa kuti bambo wa Timoteo ndi Mgriki. Pamene ankadutsa m'mizinda, ankadziŵitsa anthu mfundo zimene atumwi ndi akulu a mpingo a ku Yerusalemu aja adaapanga, nkumaŵauza kuti azisunge. Motero mipingo ya akhristu inkamangidwa pa chikhulupiriro cholima, ndipo oloŵamo ankachulukirachulukira tsiku ndi tsiku. Paulo ndi anzake aja adapitirira dera la Frijiya ndi la Galatiya, pakuti Mzimu Woyera adaaŵaletsa kulalika mau a Mulungu ku Asiya. Pamene adafika ku malire a Misiya, adayesa kuloŵa m'dera la Bitiniya, koma Mzimu wa Yesu sadaŵalole. Motero adapitirira Misiya nakafika ku Troasi. Usiku Paulo adaona m'masomphenya munthu wina wa ku Masedoniya ataima nkumampempha kuti, “Olokerani ku Masedoniya kuno, mudzatithandize.” Iye ataona zimenezi, nthaŵi yomweyo tidakonza ulendo wopita ku Masedoniya, chifukwa tidaadziŵadi kuti Mulungu ndiye watiwongolera kuti tikaŵalalikire Uthenga Wabwino anthu akumeneko. Kuchokera ku Troasi tidayenda m'chombo kulunjika ku chilumba cha Samotrase, ndipo m'maŵa mwake tidapitirira mpaka ku Neapoli. Kuchokera kumeneko tidapita ku Filipi, mzinda wa m'chigawo choyamba cha m'dera lija la Masedoniya, ndiponso boma la Aroma. Tidakhala mu mzinda umenewo masiku angapo. Pa tsiku la Sabata tidatuluka mumzindamo kupita kumtsinje kumene tinkaganiza kuti kuli malo opemphererako. Tsono tidakhala pansi nkumalankhula ndi akazi amene adaasonkhana kumeneko. Pakati pao padaali mai wina, dzina lake Lidia. Anali wa ku mzinda wa Tiatira, ndipo ntchito yake inali yogulitsa nsalu zofiirira. Anali munthu wopembedza Mulungu, ndipo Ambuye adaatsekula mtima wake kuti azisamale zimene Paulo ankanena. Iye ndi a m'banja mwake atabatizidwa, iyeyo adatipempha kuti, “Ngati mwandiwonadi kuti ndine munthu wokhulupirira Ambuye, dzaloŵeni m'nyumba mwanga, mudzakhale nafe.” Mwakuti adatikakamiza ndithu, ife nkukaloŵadi. Nthaŵi ina pamene tinkapita ku malo opemphererako, tidakumana ndi kapolo wachitsikana amene adaagwidwa ndi mzimu woipa womunenetsa zakutsogolo. Ankapindulitsa mbuye wake kwambiri ndi kulosa kwakeko. Iyeyo adayamba kutitsatira Paulo ndi ife, akufuula kuti, “Anthu aŵa ndi atumiki a Mulungu Wopambanazonse, akukulalikirani njira ya chipulumutso.” Mtsikanayo adachita zimenezi masiku ambiri. Koma Paulo zimenezo zidamunyansa, choncho adatembenuka nauza mzimu woipa uja kuti, “Iwe, m'dzina la Yesu Khristu ndikukulamula kuti utuluke mwa munthuyu.” Ndipo nthaŵi yomweyo udatulukadi. Ambuye ake a mtsikana uja ataona kuti sangapindule nayenso, adagwira Paulo ndi Silasi naŵakokera ku bwalo, kwa akulu. Atafika nawo kwa akulu oweruza milandu, adaŵauza kuti, “Anthu aŵa ndi Ayuda, ndipo akuvutitsa mumzinda mwathu. Akuphunzitsa miyambo imene ife sitiloledwa kuivomera kapena kuitsata, popeza kuti ndife Aroma.” Anthu onse adagudukira Paulo ndi Silasi, ndipo akulu oweruza milandu aja adaŵang'ambira zovala zao, nalamula kuti aŵakwapule. Ataŵakwapula kwambiri, adaŵaponya m'ndende, nalamula woyang'anira ndendeyo kuti aŵasunge bwino, angathaŵe. Chifukwa cha mau ameneŵa, woyang'anira ndende uja adakaŵatsekera m'chipinda cha m'katikati mwa ndende, namangirira mapazi ao m'matangadza. Koma pakati pa usiku Paulo ndi Silasi ankapemphera ndi kuimba nyimbo zolemekeza Mulungu, akaidi anzao nkumamvetsera. Mwadzidzidzi kudachita chivomezi champhamvu, kotero kuti maziko a ndende adagwedezeka. Nthaŵi yomweyo zitseko zonse zidatsekuka, maunyolo a mkaidi aliyense nkumasuka. Woyang'anira ndende uja atadzuka, naona kuti zitseko zonse za ndende nzotsekuka, adaayesa kuti akaidi athaŵa. Pamenepo adasolola lupanga lake nati adziphe. Koma Paulo adafuula kuti, “Iwe usadzipweteke! Tonse tilipo!” Apo woyang'anira ndende uja adaitanitsa nyale, nathamangira m'kati, ndipo ali njenjenje ndi mantha, adadzigwetsa ku mapazi a Paulo ndi Silasi. Tsono adaŵatulutsira kunja, naŵafunsa kuti, “Mabwana, Kodi ndichite chiyani kuti ndipulumuke?” Iwo adamuyankha kuti, “Khulupirira Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka iwe ndi a m'nyumba mwako.” Kenaka adamlalikira mau a Ambuye iyeyo ndi onse a m'nyumba mwake. Nthaŵi yomweyo, ngakhale unali usiku, iye adaŵatenga nakaŵatsuka mabala ao. Ndipo pompo iye pamodzi ndi onse a m'nyumba mwake adabatizidwa. Pambuyo pake adapita nawo kunyumba kwake, naŵapatsa chakudya. Ndipo iye pamodzi ndi onse a m'nyumba mwake adasangalala kwambiri chifukwa cha kukhulupirira Mulungu. M'maŵa kutacha, akulu oweruza milandu adatuma asilikali kukanena kuti, “Amasuleni anthu aja azipita.” Woyang'anira ndende uja adafotokozera Paulo mauwo, adati, “Akulu oweruza milandu atumiza mau kuti tikumasuleni. Ndiye inu tulukani, muzipita ndi mtendere.” Koma Paulo adauza asilikaliwo kuti, “Iwo aja adatikwapulira pa anthu, osaweruza mlandu wathu, chonsecho ndife nzika za ufumu wa Aroma, kenaka nkutiponya m'ndende. Ndiye tsopano akufuna kutitulutsa mobisa? Izo ndizo ai! Abwere iwowo adzatitulutse okha.” Asilikali aja adapita kukaŵafotokozera akulu oweruza milandu aja mau ameneŵa. Pamene iwo aja adamva kuti ndi nzika za ufumu wa Aroma, adachita mantha. Motero adabwera naŵapepesa, kenaka adaŵatulutsa naŵapempha kuti achokemo mumzindamo. Paulo ndi Silasi atatuluka m'ndende muja adapita kunyumba kwa Lidia. Kumeneko adaonana ndi abale, ndipo ataŵalimbikitsa, adachoka. Paulo ndi anzake aja adapitirira mizinda ya Amfipoli ndi Apoloniya nakafika ku Tesalonika. Kumeneko kunali nyumba yamapemphero ya Ayuda. Tsono Paulo adaloŵa nawo monga adaazoloŵera, ndipo adakambirana nawo za m'Malembo pa masabata atatu. Adaŵamasulira za m'Malembomo ndi kuŵatsimikizira kuti Mpulumutsi wolonjezedwa uja adaayenera kumva zoŵaŵa kenaka nkuuka kwa akufa. Paulo adati, “Yesu amene ndikukulalikiraniyu, ndiye Mpulumutsiyo.” Tsono ena mwa iwo adakopeka, natsata Paulo ndi Silasi. Agriki ambirimbiri opembedza Mulungu adateronso, pamodzi ndi akazi ambiri apamwamba. Koma Ayuda ena adachita nsanje, choncho adasonkhanitsa anthu opandapake ongoyendayenda, nayambitsa chipolowe mumzindamo. Adathamangira ku nyumba ya Yasoni, kukafuna Paulo ndi Silasi kuti aŵatulutsire ku anthu. Poona kuti sadaŵapeze, adamtenga Yasoniyo pamodzi ndi abale ena nkuŵaguzira kwa akulu amumzindamo. Tsono adafuula kuti, “Anthu aja amene akhala nasokoneza anthu ponseponse, tsopano afikanso kwathu kuno, ndipo Yasoni waŵalandira. Onseŵa akuchita zosagwirizana ndi malamulo a Mfumu ya ku Roma, pakunena kuti ati kulinso mfumu ina, dzina lake Yesu.” Mau ameneŵa adautsa mitima ya anthuwo ndi ya akulu amumzinda aja. Koma Yasoni ndi anzake aja atalipira mlanduwo, akuluwo adaŵamasula. Kutangoda, abale aja adapititsa Paulo ndi Silasi ku Berea. Atafika kumeneko, adakaloŵa m'nyumba yamapemphero ya Ayuda. Ayuda akumeneko anali a mitima yomasuka, kusiyana ndi aja a ku Tesalonika. Iwoŵa adalandira mau a Mulungu ndi mtima wofunitsitsa, ndipo tsiku ndi tsiku ankafufuza m'Malembo kuti aone ngati nzoona zimene Paulo ndi Silasi ankanena. Motero mwa iwowo ambiri adakhulupirira, ndiponso Agriki ambiripo, akazi apamwamba ndi amuna omwe, adakhulupirira. Koma Ayuda a ku Tesalonika aja atamva kuti Paulo adalalika mau a Mulungu ndi ku Berea komwe, adakafika komwekonso, nayamba kukolezera ndi kuutsa mitima ya anthu. Nthaŵi yomweyo abale aja adatuma anthu ena kuti aperekeze Paulo ku nyanja, koma Silasi ndi Timoteo adakhalira komweko. Anthu amene adaaperekeza Paulo aja adakafika naye mpaka ku Atene. Pambuyo pake adabwerera ku Berea, Paulo ataŵalamula kukauza Silasi ndi Timoteo kuti amlondole msanga. Pamene Paulo ankadikira Silasi ndi Timoteo ku Atene, mtima wake udavutika kwambiri poona kuti mzinda wonse ngwodzaza ndi mafano. Tsono adakambirana m'nyumba yamapemphero ndi Ayuda ndi anthu ena opembedza Mulungu. Adakambirananso ndi anthu amene ankangokumana nawo pa msika tsiku ndi tsiku. Anzeru enanso a magulu a Aepikurea ndi Astoiki adadzatsutsana naye. Ena ankati, “Kodi mbutuma yolongololayi ikufunanso kunena chiyani?” Enanso ankati, “Ameneyu akukhala ngati wolalika za milungu yachilendo.” Ankanena zimenezi chifukwa iye ankalalika Uthenga Wabwino wonena za Yesu, ndi za kuuka kwa akufa. Tsono adapita naye ku bwalo lamilandu lotchedwa Areopagi, namuuza kuti, “Ife timati mutidziŵitseko zatsopano zimene mukuphunzitsazi? Pakuti zina zimene mukutiwuzazi nzachilendo, ndipo tikufuna kudziŵa kuti zinthuzi nzotani.” Ndiye kuti nzika za ku Atene ndi alendo okhala kumeneko, inali ngati ntchito nthaŵi zonse kumangomvera zatsopano ndi kumazifotokozera. Paulo adaimirira pakati pa bwalo lija la Aeropagi nati, “Inu anthu a ku Atene, pa zonse ndikuwona kuti ndinu anthu opembedza kwambiri. Pakuti pamene ndinalikuyenda mumzindamu, nkumaona malo anu osiyanasiyana achipembedzo, ndinapezanso guwa lina lansembe pamene padalembedwa mau akuti, ‘Kwa Mulungu wosadziŵika.’ Tsonotu amene mumampembedza osamdziŵayo, ndi yemweyo amene ine ndikukulalikirani. Mulungu amene adalenga dziko lapansi ndiponso zonse zili m'menemo, ndiye Mwini Kumwamba ndi dziko lapansi. Iye sakhala m'nyumba zachipembedzo zomangidwa ndi anthu ai. Anthu sangamtumikire ndi manja ao, ngati kuti Iye amasoŵa kanthu. Pajatu Iye ndiye amapatsa anthu onse moyo, mpweya ndi zina zonse. Kochokera mwa kholo limodzi Iye adalenga mitundu yonse ya anthu, kuti ikhale pa dziko lonse lapansi. Adakonzeratu nthaŵi ya moyo wao, ndiponso malire a pokhala pao. Mulungu adafuna kuti anthu amufunefune, ndipo kuti pomfufuzafufuza, mwina nkumupeza. Komabe Iye sali kutali ndi aliyense mwa ife. Paja “ ‘Mwa Iye ife timakhala ndi moyo, timayenda ndipo timakhala tilipo.’ Monga adanenera opeka ndakatulo anu ena kuti, “ ‘Ifenso ndife ofumira mwa Iye ngati ana ake.’ “Tsono popeza kuti tili ngati ana a Mulungu, sitiyenera kuganiza kuti umulungu wake umafanafana ndi fano lagolide kapena lasiliva kapena lamwala, lopangidwa mwa luso ndi nzeru za munthu. Mulungu adaaŵalekerera anthu pa nthaŵi imene iwo anali osadziŵa, koma tsopano akuŵalamula anthu onse ponseponse kuti atembenuke mtima. Chifukwa adaika tsiku pamene Iye adzaweruza anthu a pa dziko lonse lapansi molungama kudzera mwa Munthu amene Iye adamsankha. Adatsimikizira anthu onse zimenezi pakuukitsa Munthuyo kwa akufa.” Pamene anthuwo adamva za kuuka kwa akufa, ena adangoseka. Koma ena adati, “Bwanji mudzatiwuzenso zimenezi tsiku lina.” Choncho Paulo adaŵasiya. Koma ena adamtsata, nakhulupirira. Pakati pao panali Dionizio, mmodzi mwa a bwalo la milandu lotchedwa Areopagi, ndiponso mai wina, dzina lake Damalisi, ndi enanso. Pambuyo pake Paulo adachoka ku Atene napita ku Korinto. Kumeneko adapezako Myuda wina, dzino lake Akwila, mbadwa ya ku Ponto. Iye anali atangofika chatsopano kuchokera ku Italiya pamodzi ndi mkazi wake Prisila, chifukwa Klaudio, Mfumu ya ku Roma, adaalamula kuti Ayuda onse achoke ku Roma. Tsono Paulo adapita kukaŵaona. Ndiye popeza kuti iwo anali amisiri a ntchito imodzimodzi ngati yake, yosoka mahema, iyeyo adakhala nawo namagwirira limodzi ntchito. Pa tsiku la Sabata lililonse iye ankakambirana ndi anthu ku nyumba yamapemphero ya Ayuda, namayesetsa kukopa Ayuda ndi Agriki omwe. Silasi ndi Timoteo atafika kuchokera ku Masedoniya, Paulo tsopano ankangogwira ntchito yolalikira, ndi kuŵauza Ayuda monenetsa kuti Yesu ndiye anali Mpulumutsi wolonjezedwa uja. Koma pakuti iwo adaatsutsana naye ndi kumchita chipongwe, Paulo adalekana nawo pakukutumula zovala zake, naŵauza kuti, “Mwadziphetsa ndi mtima wanu. Tsono izo nzanu, ine ndilibe chifukwa. Kuyambira tsopano ndipita kwa akunja.” Motero adachoka kumeneko napita ku nyumba ya munthu wina, dzina lake Tito Yusto. Iyeyu anali munthu wopembedza Mulungu, ndipo nyumba yake idaayandikana ndi nyumba yamapemphero. Krispo, mkulu wa nyumba yamapempheroyo pamodzi ndi onse a pa banja lake adakhulupirira Ambuye. Ndipo anthu ambiri a ku Korinto atamva mau a Paulo, adakhulupirira nabatizidwa. Tsiku lina usiku Ambuye adaonekera Paulo m'masomphenya namuuza kuti, “Usaope, koma upitirire kulalika, osakhala chete ai, pakuti Ine ndili nawe pamodzi. Palibe munthu adzakukhudza kuti akuchite choipa, ndipo ndili nawo anthu ambiri mumzinda muno.” Choncho Paulo adakhala komweko chaka chimodzi ndi miyezi isanu ndi umodzi, akuŵaphunzitsa mau a Mulungu. Pamene Galio anali bwanamkubwa wa ku Akaiya, Ayuda onse pamodzi adaukira Paulo, namtengera ku bwalo la milandu. Iwo adati, “Munthu uyu akukopa anthu kuti azipembedza Mulungu mwa njira zotsutsana ndi Malamulo athu.” Koma pamene Paulo adati azilankhula, Galio adauza Ayuda kuti, “Ukadakhala mlandu wakuti munthu wachimwira lamulo, kapena wakuti walakwira mnzake, bwenzi nditakumverani bwinobwino, Ayuda inu. Koma popeza kuti ndi nkhani yokhudza mau, ndi maina, ndiponso Malamulo anu, mudziwonere nokha. Kuti ndiweruze zimenezi, ine toto.” Atatero adaŵapirikitsa kubwaloko. Pamenepo onsewo adagwira Sostene, mkulu wa nyumba yamapemphero ya Ayuda, nammenyera m'bwalo momwemo. Koma Galio sadasamaleko zimenezi. Paulo adakhalabe ku Korinto masiku ambiri. Pambuyo pake adalaŵirana ndi abale, naloŵa m'chombo kupita ku Siriya pamodzi ndi Prisila ndi Akwila. Asanaloŵe m'chombomo, Paulo adameta tsitsi lake ku Kenkrea, chifukwa anali atachita lumbiro kwa Mulungu. Iwo adakafika ku Efeso, ndipo kumeneko Paulo adasiyako Akwila ndi Prisila. Koma iye yekha adaloŵa m'nyumba yamapemphero nakambirana ndi Ayuda. Pamene ameneŵa adampempha kuti akhale nawo nthaŵi yaitali, iye sadavomere. Adaŵatsazika naŵauza kuti, “Mulungu akalola ndidzabweranso.” Atatero adachoka ku Efeso m'chombo. Pamene adafika ku Kesareya, adapita ku Yerusalemu kukacheza pang'ono ndi mpingo. Kuchokera kumeneko adapita ku Antiokeya. Atakhala kumeneko kanthaŵi ndithu, adachokako nakayendera dziko la Galatiya ndi la Frijiya, akulimbikitsa ophunzira onse. Myuda wina, dzina lake Apolo, mbadwa ya ku Aleksandriya, adabwera ku Efeso. Anali munthu wodziŵa kulankhula ndi wodziŵa Malembo kwambiri. Iyeyu adaaphunzitsidwa Njira ya Ambuye, ndipo ndi changu chachikulu ankalankhula ndi kuphunzitsa za Yesu molongosoka, chonsecho ankangodziŵa za ubatizo wa Yohane wokha. Tsono adayamba kulankhula molimba mtima m'nyumba yamapemphero ya Ayuda. Koma pamene Prisila ndi Akwila anamumva, adamtenga namufotokezera Njira ya Mulungu molongosoka koposa. Pamene Apolo adafuna kuwolokera ku Akaiya, abale adamlimbikitsa, nalembera ophunzira akumeneko kalata kuti amlandire bwino. Tsono atafikako, adaŵathandiza kwambiri amene anali atakhulupirira chifukwa cha kukoma mtima kwa Mulungu. Pakuti iye adaatsutsa Ayuda mwamphamvu pamaso pa anthu, natsimikiza ndi Malembo kuti Yesu ndiyedi Mpulumutsi wolonjezedwa uja. Pamene Apolo anali ku Korinto, Paulo adayendera maiko apamtunda, nakafika ku Efeso. Kumeneko adapezako ophunzira ena, ndipo adaŵafunsa kuti, “Kodi mudalandira Mzimu Woyera pamene mudakhulupirira?” Iwo adati, “Nkumva komwe sitinamve kuti kuli Mzimu Woyera.” Paulo adaŵafunsa kuti, “Nanga tsono mudabatizidwa ndi ubatizo wotani?” Iwo adati, “Ndi ubatizo wa Yohane.” Paulo adati, “Yohane ankabatiza anthu otembenuka mtima, koma iye yemwe ankauza anthuwo kuti akhulupirire wina amene analikudza pambuyo pa iyeyo. Winayo ndiye Yesu.” Okhulupirira aja atamva zimenezi, adabatizidwa m'dzina la Ambuye Yesu. Pamene Paulo adaŵasanjika manja, Mzimu Woyera adadza pa iwo, ndipo adayamba kulankhula zilankhulo zosadziŵika, ndi kumalalika mau ochokera kwa Mulungu. Anthuwo onse pamodzi analipo ngati khumi ndi aŵiri. Paulo adaloŵa m'nyumba yamapemphero ya Ayuda, ndipo pa miyezi itatu adakhala akulankhula molimba mtima. Ankakamba ndi anthu za ufumu wa Mulungu, nayesa kuŵakopa. Koma ena adaumitsa mitima yao, osafuna kukhulupirira, nkumanyoza Njira ya Ambuye pamaso pa gulu lonse. Pamenepo Paulo adaŵasiya nachoka nawo ophunzira aja, ndipo tsiku ndi tsiku ankakambirana m'sukulu ya Tirano. Adachita zimenezi pa zaka ziŵiri, kotero kuti anthu onse okhala ku Asiya, Ayuda ndi Agriki omwe, adamva mau a Ambuye. Mulungu adachita zozizwitsa kwambiri kudzera kwa Paulo. Anthu ankati akatenga zitambaya kapena nsalu zina zimene Paulo ankagwiritsa ntchito, nakaziika pa anthu odwala, odwalawo ankachira, ndipo mizimu yoipa inkatuluka mwa iwo. Ayuda ena oyendayenda, otulutsa mizimu yoipa, nawonso adayesa kutchula dzina la Ambuye Yesu pa anthu ogwidwa ndi mizimu yoipa. Ankati, “M'dzina la Yesu amene Paulo amamlalika, ndikukulamulani kuti mutuluke.” Amene ankachita zimenezi ndi ana aamuna asanu ndi aŵiri a Skeva, mkulu wa ansembe onse wachiyuda. Koma mzimu woipawo udayankha kuti, “Yesu ndimamdziŵa, Paulonso ndimamdziŵa, koma inuyo ndinu yani?” Kenaka munthu wogwidwa ndi mizimu yoipa uja adaŵalumphira naŵagwira onse. Adaŵagonjetsa kotero kuti iwowo adathaŵanso m'nyumba muja ali maliseche ndiponso atapwetekedwa. Anthu onse okhala ku Efeso, Ayuda ndi Agriki atamva zimenezi, adachita mantha. Ndipo anthu ankatamanda dzina la Ambuye Yesu kopambana. Ambiri amene tsopano adaayamba kukhulupirira, adabwera nkumavomera poyera ndi kuulula zoipa zimene ankachita. Ambiri amene ankakonda kuchita matsenga, adasonkhanitsa mabuku ao naŵatentha pamaso pa anthu onse. Pamene adaonkhetsa mtengo wa mabukuwo, adapeza kuti udaakwanira ngati ndalama zikwi makumi asanu. Motero mau a Mulungu adanka nafalikirafalikira ndi kugwira ntchito mwamphamvu. Zitachitika zimenezi, Paulo adatsimikiza zopita ku Yerusalemu kudzera ku Masedoniya ndi ku Akaiya. Adati, “Kuchokera kumeneko ndiyeneranso kukayenda ku Roma.” Tsono adatuma Timoteo ndi Erasito ku Masedoniya. Ameneŵa anali aŵiri mwa anthu omuthandiza. Koma mwiniwakeyo adakhalirabe ku Asiya kanthaŵi. Nthaŵi yomweyo padabuka chipolowe chachikulu chifukwa cha Njira ya Ambuye. Mmisiri wina wa ntchito za siliva, dzina lake Demetrio, ankapanga timafanizo tasiliva ta nyumba yopembedzeramo Aritemi, mulungu wao wamkazi, ndipo ntchito yakeyo inkaŵapindulitsa kwambiri antchito ake. Demetrioyo adasonkhanitsa anthu akewo, pamodzi ndi ena ogwira ntchito ya mtundu womwewo, naŵauza kuti, “Abale anga, mukudziŵa kuti chuma chathu chimachokera ku ntchito imeneyi. Mukuwona ndi kumva zimene akuchita mkulu uyu amati Pauloyu. Iye akunena kuti ati milungu yopangidwa ndi anthu si milungu konse. Ndipo wakopa anthu ambiri nkuŵapatutsa, osati ku Efeso kokha kuno ai, komanso pafupi dziko lonse la Asiya. Tsono choopsa nchakuti ntchito yathuyi ifika ponyozeka. Si pokhapo ai, komanso nyumba yopembedzeramo Aritemi, mulungu wathu wamkulu, anthu sadzaiyesa kanthu. Ndiye basitu udzawonongeka ulemerero wonse wa Aritemiyo, amene anthu onse a ku Asiya ndi a pa dziko lonse lapansi amampembedza.” Anthu aja atamva mau ameneŵa, adakwiya kwabasi, nayamba kufuula kuti, “Ndi wamkulu Aritemi wa Aefeso!” Choncho mumzinda monse mudadzaza chisokonezo. Tsono anthuwo adagwira Gayo ndi Aristariko, anthu a ku Masedoniya, anzake aulendo a Paulo, nathamangira nawo ku bwalo lamaseŵera. Paulo adaafuna kuloŵa pakati pa anthuwo, koma ophunzira sadamloleze. Akulu ena a Boma a ku Asiya komweko, amene anali abwenzi ake, adamtumiranso mau omupempha kuti asaloŵe dala m'bwalo lamaseŵeralo. Msonkhano wonse wa anthu aja udangoti pwirikiti: ena akufuula zina, enanso zina; ambiri osadziŵa ndi chimene asonkhanira chomwe. Ena m'khamumo adaaganiza kuti Aleksandro alipo ndi chonena, ataona kuti Ayuda amkankhira kutsogolo. Tsono iye adakweza dzanja kuti aŵakhalitse chete, kuti afotokozere anthu mlanduwo. Koma pamene anthu aja adazindikira kuti iyeyo ndi Myuda, onsewo adafuula pamodzi pa maola aŵiri kuti, “Ndi wamkulu Aritemi wa Aefeso!” Mlembi wa mzindawo ataŵatontholetsa anthu aja, adaŵauza kuti, “Inu Aefeso, ndani amene sadziŵa kuti mzinda wa Aefeso ndiwo wosunga nyumba yopembedzeramo Aritemi wamkulu, ndiponso wosunga mwala wopatulika uja umene udachita kugwa kuchokera kumwamba? Tsono popeza kuti palibe amene angatsutse zimenezi, inu muyenera kukhala chete, osachita zinthu mopupuluma. Inu mwabwera ndi anthu aŵa kuno, ngakhale iwo sadabe za m'nyumba ya mulungu wathu wamkazi, kapena kumchita chipongwe. Ngati Demetrio ndi amisiri anzake ali ndi kanthu ndi munthu wina, mabwalo amilandu alipo, oweruza aliponso. Akakambirane milandu yao komweko. Koma ngati mukufunanso kanthu kena, kameneko msonkhano waulamuliro wa anthu onse ndiwo ukatsirize. Pakuti pali choopsa chakuti tingathe kuimbidwa mlandu wochita chipolowe chifukwa cha zimene zachitika lerozi. Palibe chifukwa chilichonse cha chipolowechi, ndipo tikasoŵa ponena akatifunsa.” Atanena zimenezi, adauza anthu aja kuti azipita. Phokoso lija litatha, Paulo adaitanitsa ophunzira aja, naŵalimbitsa mtima. Ndipo atatsazikana nawo, adachoka napita ku Masedoniya. Adayendera madera a komweko nalimbitsa mtima anthu ndi mau ambiri. Pambuyo pake adapita ku Grisi, nakakhalako miyezi itatu. Pamene anali pafupi kupita ku Siriya pa chombo, Ayuda adamchita chiwembu. Tsono iye adatsimikiza zodzera ku Masedoniya. Adamperekeza ndi Sopatere, mwana wa Piro, wa ku Berea; Aristariko ndi Sekundo a ku Tesalonika; Gayo wa ku Deribe; Timoteo; ndi Tikiko ndi Trofimo a ku Asiya. Iwoŵa adatsogola nakatidikira ku Troasi. Koma ife tidayenda pa chombo kuchokera ku Filipi, itatha Paska, chikondwerero cha mikate yosafufumitsa. Ndipo patapita masiku asanu, tidakumana nawo ku Troasi. Kumeneko tidakhalako masiku asanu ndi aŵiri. Pa tsiku loyamba la sabata, tidasonkhana kuti tidye Mgonero, ndipo Paulo ankakamba ndi anthu. Popeza kuti ankayembekeza kupita m'maŵa mwake, adapitiriza kulankhula mpaka pakati pa usiku. M'chipinda cham'mwamba chimene tidaasonkhanamo munali nyale zambiri. Mnyamata wina, dzina lake Yutiko, adaakhala pa windo. Tsono Paulo akukambabe ndi anthu aja, Yutikoyo ankaodzera kwambiri, mpaka adagona tulo ndithu, nagwa pansi kuchokera pa nyumba yam'mwamba. Ndipo adamtola ali wakufa. Pamenepo Paulo adatsika, nadziponya pa mnyamatayo nkumufungatira nati, “Musavutike, ali moyo.” Kenaka Paulo adakweranso, nakanyema nao mkate, nkudya nao. Pambuyo pake adapitiriza kulankhula nao nthaŵi yaitali, nangochoka kutacha kale. Anthu aja adatenga mnyamata uja ali moyo, ndipo onse adasangalala kwambiri. Ife tidatsogola nkukakwera chombo kupita ku Aso, kumene tinkayembekeza kukatengako Paulo. Iye adaakonza motero, chifukwa adaafuna kudzera pa mtunda. Pamene iye adakumana nafe ku Aso, adakwera nafe m'chombomo, ndipo tidakafika ku Mitilene. Tidachokanso kumeneko m'chombo, ndipo m'maŵa mwake tidakafika pafupi ndi Kiyo. M'maŵa mwakenso tidawolokera ku Samo, ndipo mkucha wake tidakafika ku Mileto. Paulo anali atatsimikiza zolambalala Efeso, kuwopa kutaya nthaŵi ku dziko la Asiya. Ankafulumira kuti ngati nkotheka akakhale ali ku Yerusalemu pa tsiku la Pentekoste. Paulo ali ku Mileto, adatumiza mau ku Efeso kuitana akulu a mpingo. Iwo atafika, adaŵauza kuti, “Inu nomwe mukudziŵa m'mene ndidakhalira nanu masiku onse, kuyambira tsiku loyamba lija ndidafika ku Asiya. Ndinkatumikira Ambuye modzichepetsa kwenikweni, pakati pa chisoni ndi zovuta zimene zidandigwera chifukwa cha ziwembu za Ayuda. Mukudziŵa kuti sindidakubisireni kanthu kalikonse koti nkukuthandizani. Ndidakulalikirani ndi kukuphunzitsani poyera ndiponso m'nyumba zanu. Ayuda ndi Agriki omwe ndidaŵapempha kolimba kuti atembenukire kwa Mulungu molapa, ndi kumakhulupirira Ambuye athu Yesu. “Ndipo tsopano, onani ndikupita ku Yerusalemu, popeza kuti Mzimu Woyera akundilamula. Zimene zikandigwere kumeneko sindikuzidziŵa konse. Chokhachi ndikudziŵa kuti Mzimu Woyera wandichenjeza mu mzinda uliwonse kuti ndende ndi mazunzo zikundidikira. Koma sindilabada konse za moyo wanga, ngati kuti ndi wa mtengo wapatali kwa ine, malinga ndikatsirize ntchito yanga, ndi utumiki umene Ambuye Yesu adandipatsa, ndiye kuti kulalika poyera Uthenga Wabwino wonena za kukoma mtima kwa Mulungu. “Tsopano ndikudziŵa kuti inu nonse amene ndidakuyenderani kumakulalikirani za ufumu wa Mulungu, simudzaonanso nkhope yanga ai. Nchifukwa chake ndikukuuzani monenetsa lero, kuti ngati ena mwa inu atayike, izo nzao, ine ndilibepo mlandu. Pajatu sindidakubisireni kanthu ai, koma ndidakulalikirani zonse zimene Mulungu afuna. Mzimu Woyera adakuikani kuti muziyang'anira mpingo wonse. Tsono mudzisamale nokha, ndipo musamalenso mpingowo. Ŵetani nkhosa za mpingo wa Ambuye umene Iwo adauwombola ndi magazi aoao. Ndikudziŵa kuti ndikadzachoka ine, padzaloŵa mimbulu yoopsa pakati panu, imene siidzalekerera nkhosazo. Ngakhale pakati pa inu nomwe, padzauka ena olankhula zonama nkumakopa ophunzira kuti aŵatsate. Ndiye inu khalani maso. Kumbukirani kuti pa zaka zitatu usana ndi usiku sindidaleke kulangiza aliyense mwa inu ndi misozi. “Choncho tsopano ndikukuikani m'manja mwa Mulungu, mau ake oonetsa kukoma mtima kwake akusungeni bwino. Mauwo ali ndi mphamvu zakukulitsa mpingo, ndi kukupatsani madalitso onse aja amene Mulungu akusungira anthu ake. Sindidasirire ndalama kapena zovala za munthu aliyense ai. Inu nomwe mukudziŵa kuti manja angaŵa adagwira ntchito kuti ndipeze zimene ine ndi anzanga tinkasoŵa. Pa zonse ndakuwonetsani kuti pakugwira ntchito kolimba motere, tiyenera kuthandiza ofooka. Kumbukirani mau aja a Ambuye Yesu akuti, ‘Kupatsa kumadalitsa munthu koposa kulandira.’ ” Paulo atanena zimenezi, adagwada pansi napemphera nawo pamodzi ena onse aja. Onsewo adalira kwambiri. Adamkumbatira Pauloyo namumpsompsona polaŵirana naye. Makamaka adachita chisoni chifukwa cha mau ake aja onena kuti iwo sadzaonanso nkhope yake. Pambuyo pake adamperekeza kuchombo. Titalaŵirana nawo, tidachoka kumeneko m'chombo, ndipo tidayenda molunjika kukafika ku Kosi. M'maŵa mwake tidakafika ku Rode, ndipo kuchokera kumeneko tidakafika ku Patara. Kumeneko tidapeza chombo chopita ku Fenisiya. Tsono tidaloŵamo nkunyamuka. Tidaona chilumba cha Kipro, koma tidachisiya ku dzanja lamanzere nkupita ku Siriya. Tidakafika ku Tiro, popeza kuti chombo chinkayenera kukatsitsa katundu kumeneko. Tidafunafuna ophunzira akumeneko, ndipo titaŵapeza, tidakhala nawo masiku asanu ndi aŵiri. Ndi chiwongolero cha Mzimu Woyera iwo aja adauza Paulo kuti asapite ku Yerusalemu. Koma pamene masiku athu aja adatha, tidachokako nkupitirira ulendo wathu. Onsewo, pamodzi ndi akazi ao ndi ana awo omwe, adatiperekeza mpaka kunja kwa mzinda. Tidagwada pa mchenga m'mbali mwa njanja nkupemphera. Ndipo titatsazikana, ife tidakaloŵa m'chombo, iwowo nkumabwerera kwao. Tidapitirira ulendo wathu wochokera ku Tiro mpaka tidakafika ku Ptolemaisi. Kumeneko tidacheza pang'ono ndi abale, nkukhala nawo tsiku limodzi. M'maŵa mwake tidanyamuka nkukafika ku Kesareya. Tidapita kunyumba kwa mlaliki Filipo, mmodzi mwa atumiki a mpingo asanu ndi aŵiri aja, ndipo tidakhala kunyumba kwakeko. Iyeyo anali ndi ana aakazi anai osakwatiwa, amene ankalalika uthenga wa Mulungu. Ife tili kumeneko masiku angapo, kudabwera mneneri wina kuchokera ku Yudeya, dzina lake Agabu. Iyeyo adadza kwa ife, ali ndi lamba wa Paulo. Tsono adadzimanga mapazi ndi manja nati, “Mzimu Woyera akuti, ‘Mwiniwake lamba uyu Ayuda adzammanga chomwechi ku Yerusalemu, ndi kumpereka m'manja mwa akunja.’ ” Titamva zimenezi, ife pamodzi ndi athu akumeneko tidampemphha Paulo kuti asapite ku Yerusalemu. Koma iye adati, “Bwanji mukulira ndi kufuna kunditayitsa mtima? Inetu ndili wokonzeka kumangidwa, ngakhalenso kukafera ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu.” Tsono popeza kuti adaatikanika ndithu, tidangomuleka nkunena kuti, “Zichitike zimene Ambuye akufuna.” Masiku athu okhala kumeneko atatha, tidakonza ulendo wathu ndipo tidapita ku Yerusalemu, Ophunzira ena a ku Kesareya nawonso adatsagana nafe. Adakatitula kunyumba kwa munthu wina, dzina lake Mnasoni, kumene adaakonza kuti tizikakhala. Iyeyu anali wa ku Kipro, ndipo anali wophunzira wakalekale. Titafika ku Yerusalemu, abale adatilandira ndi chimwemwe. M'maŵa mwake Paulo adatitenga kupita kwa Yakobe. Akuluampingo onse anali kumeneko. Atalonjerana nawo, Paulo adaŵafotokozera mwatsatanetsatane zonse zimene Mulungu adaachita pakati pa anthu a mitundu ina kudzera mu utumiki wake. Pamene iwo adamva zimenezi, adayamika Mulungu. Ndipo adauza Paulo kuti, “Inu mbale wathu, mukuwona kuti pali Ayuda ambirimbiri amene asanduka okhulupirira. Onsewo ngokhulupirika kwambiri pa kutsata Malamulo a Mose. Anthu aŵauza za inu kuti Ayuda onse okhala ku maiko achilendo, inu mumaŵaphunzitsa kuti alekane nawo Malamulowo. Akutinso mumaŵaphunzitsa kuti asamaumbale ana ao kapena kusamala miyambo yachiyuda. Tsono pamenepa titani? Kumva adzamva ndithu kuti mwafika. Ndiye inu, muchite zimene tikuuzeni ife. Tili ndi amuna anai pano amene adachita lumbiro kwa Mulungu. Muŵatenge ndipo muchite nawo mwambo wakudziyeretsa. Tsono muŵalipirire zoti apereke ku Nyumba ya Mulungu kuti amete tsitsi lao. Mukatero, anthu onse adzadziŵa kuti si zoona zimene anthu adaŵauza za inu, koma kuti inu mumasamala ndithu Malamulo a Mose. Koma kunena za anthu a mitundu ina amene adasanduka okhulupirira, ife taŵalembera kalata yoŵauza zimene tidavomerezana: kuti asamadye chakudya chimene chidaperekedwa nsembe ku mafano, asamadye magazi kapena nyama yochita kupotola, ndiponso asamachite dama.” Pamenepo Paulo adaŵatenga anthu anai aja, ndipo m'maŵa mwake adachita nawo mwambo wakudziyeretsa. Iyeyo adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu nakadziŵitsa ansembe za tsiku loti aliyense mwa iwo adzamperekere nsembe, atatha masiku akudziperekawo. Atatha masiku asanu ndi aŵiri aja, Ayuda ochokera ku Asiya adaona Paulo m'Nyumba ya Mulungu. Adautsa mitima ya anthu onse, namgwira. Tsono iwo adafuula kuti, “Inu Aisraele, tithandizeni! Ndi uyutu munthu uja amene akuphunzitsa anthu ponseponse zonyoza mtundu wathu, Malamulo a Mose ndiponso malo ano. Kuwonjezera apo waloŵetsanso akunja m'Nyumba ya Mulungu muno, ndi kudetsa malo athu opatulikaŵa.” Adanena zimenezi chifukwa anali ataona Trofimo wa ku Efeso ali ndi Paulo mumzindamo, ndiye iwo ankaganiza kuti Paulo ndiye adaamloŵetsa m'Nyumba ya Mulungu. Tsono mumzinda monse mudaloŵa chisokonezo ndipo anthu onse adathamangira pamodzi namgwira Pauloyo. Adamkokera kunja kwa Nyumba ya Mulungu, nkutseka pa makomo nthaŵi yomweyo. Pamene anthu aja ankafuna kupha Paulo, mkulu wa gulu lonse la asilikali achiroma adalandira mau akuti mu mzinda wonse wa Yerusalemu muli chipolowe. Pompo iye adatenga asilikali ndi atsogoleri a magulu a asilikali, nathamangira anthu aja. Pamene anthuwo adaona mkulu wa asilikaliyo ndi asilikali aja, adaleka kummenya Paulo. Pamenepo mkulu wa asilikali uja adafika nagwira Paulo, nkulamula kuti ammange ndi maunyolo aŵiri. Kenaka adafunsa kuti, “Kodi munthuyu ndani? Ndipo watani kodi?” Koma pakati pa anthuwo ena adayamba kufuula zina, ena zina. Chifukwa cha phokosolo mkulu wa asilikali uja sadathe kudziŵa kuti zoona zenizeni nziti. Choncho adalamula kuti amtenge Pauloyo apite naye ku linga la asilikali. Tsono pamene adafika pa makwerero a kulingako, asilikali aja adachita kumnyamula, chifukwa chakuti anthuwo adaalusa zedi. Onsewo ankaŵatsatira akufuula kuti, “Mupheni basi.” Ali pafupi kuloŵa naye m'lingamo, Paulo adapempha mkulu wa asilikali uja kuti, “Kodi mungandilole kuti ndikuuzeni kanthu?” Iye adati, “Kani umalankhula Chigriki? Tsono ndiye kuti sindiwe Mwejipito uja udautsa chipolowe masiku apitawo nkutsogolera zigaŵenga zikwi zinai kupita nazo ku chipululu?” Paulo adayankha kuti, “Inetu ndine Myuda, nzika ya ku Tariso, mzinda wotchuka wa ku Silisiya. Ndikukupemphani tsono, mundilole kuti ndilankhule nawo anthuŵa.” Adamloladi, ndipo Paulo adaima pamakwerero paja, naweyula dzanja kuti anthuwo akhale chete. Pamene onse adakhala chete, Paulo adayamba kulankhula nawo pa Chiyuda. Adati, “Inu abale anga ndi inu akuluakulu, mvereni ndiyankhe tsopano zimene akundinenezazi.” Pamene iwo adamumva akulankhula nawo pa Chiyuda, adakhala chete kopambana. Tsono Paulo anati, “Inetu ndiye Myuda mbadwa ya ku Tariso, mzinda wa ku Silisiya, koma ndidaleredwa mu mzinda wa Yerusalemu mom'muno. Gamaliele ndiye anali mphunzitsi wanga amene adandiphunzitsa kwenikweni kusunga Malamulo a makolo athu. Ndipo ndinkalimbikira kwambiri pa za Mulungu, monga momwe mukuchitira nonsenu lero lino. Ndinkazunza anthu otsata Njira Yatsopanoyi, mpaka kumaŵapha. Ndinkaŵagwira anthuwo amuna ndi akazi omwe, nkumaŵamangitsa. Mkulu wa ansembe onse ndi onse a m'Bungwe la akuluakulu a Ayuda angathe kundivomereza. Iwowo adaandipatsa makalata opita nawo kwa abale athu achiyuda ku Damasiko. Tsono ndidapita komweko kuti ndikaŵagwire anthu ameneŵa, ndi kubwera nawo ku Yerusalemu ali omangidwa, kuti adzalangidwe.” “Pamene ndinali pa ulendowo ndi kuyandikira Damasiko, nthaŵi ili ngati 12 koloko yamasana, mwadzidzidzi kuŵala kwakukulu kochokera kumwamba kudandizinga. Ndidagwa pansi kenaka ndidamva mau onena kuti, ‘Saulo, Saulo, ukundizunziranji?’ Ine ndidafunsa kuti, ‘Ndinu yani, Ambuye?’ Ndipo iwo adati, ‘Ine ndine Yesu wa ku Nazarete, amene iwe ukumzunza.’ Anzanga apaulendo adaakuwona kuŵalako, koma mau a amene ankalankhula naneyo sadaŵamve. Tsono ine ndidafunsa kuti, ‘Ndichite chiyani, Ambuye?’ Ndipo Ambuye adati. ‘Dzuka, pita ku Damasiko, kumeneko akakuuza zonse zimene Mulungu wakonza kuti ukachite.’ Sindidathe kupenyanso chifukwa cha kuŵala kwakukulu kuja, nchifukwa chake anzanga aja adachita kundigwira pa dzanja nkumanditsogolera mpaka kukaloŵa m'Damasiko. “Kumeneko kunali munthu wina, dzina lake Ananiya. Anali munthu woopa Mulungu ndi wosamala Malamulo athu, ndipo Ayuda onse akumeneko ankamutama. Iyeyo adafika nadzaimirira pafupi nane, nkundiwuza kuti, ‘Mbale wanga Saulo, yambanso kupenya.’ Nthaŵi yomweyo ndidayambadi kupenya ndipo iyeyo ndidamuwona. Tsono adandiwuza kuti, ‘Mulungu wa makolo athu adakusankha kuti udziŵe zimene Iye akufuna, uwone Wolungama uja, ndipo umve mau ake olankhula nawe. Pakuti udzamchitira umboni kwa anthu onse pa zimene waziwona ndi kuzimva. Nanga tsono ukuchedweranji? Dzuka ndi kutama dzina lake mopemba, ubatizidwe ndi kusambitsidwa kuti machimo ako achoke.’ ” “Tsono ndidabwerera ku Yerusalemu, ndipo pamene ndinkapemphera m'Nyumba ya Mulungu, ndidachita ngati ndakomoka. Ndidaona Ambuye akundiwuza kuti, ‘Fulumira, tuluka msangamsanga m'Yerusalemu muno, chifukwa anthuŵa sadzauvomera umboni wako wonena za Ine.’ Ine ndidati, ‘Zoonadi Ambuye, chifukwa iwo omwe akudziŵa kuti ine ndinkapita ku nyumba iliyonse yamapemphero kukaŵagwira ndi kuŵaponya m'ndende, nkumaŵakwapula onse okhulupirira Inu. Pamene ankapha Stefano, mboni yanu, inenso ndinali pomwepo. Ndinkavomerezana nawo, ndipo ndinkasunga ndine zovala za amene ankamuphawo.’ Apo Ambuye adandiwuza kuti, ‘Nyamuka, chifukwa Ine ndidzakutuma kutali kwa anthu a mitundu ina.’ ” Mpaka apa anthu aja ankamvetsera bwinobwino mau a Paulo. Koma pamene adadzatchula mau otsirizaŵa, iwo adayamba kufuula kuti, “Munthu wotere koma kungokonzeratu. Sayeneranso kukhala moyo.” Iwowo ankafuula nkumazunguza malaya ao, namawaza fumbi kumwamba. Nthaŵi yomweyo mkulu wa asilikali uja adalamula kuti aloŵe naye Paulo m'linga la asilikali lija. Adaŵauza kuti amkwapule, kuti iyeyo aulule chifukwa chimene anthu aja ankamukuwizira chotere. Pamenepo padaaimirira mtsogoleri wa gulu la asilikali 100. Tsono asilikali ake atamanga Paulo kuti amkwapule, Pauloyo adafunsa kuti, “Kodi malamulo anu amalola kukwapula mfulu yachiroma musanazenge nkomwe mlandu wake?” Pamene mtsogoleriyo adamva zimenezi, adapita kwa mkulu wa asilikali uja namufunsa kuti, “Kodi inu mukuti mutani? Munthu ujatu ndi mfulu yachiroma.” Apo mkuloyo adadzafunsa Paulo kuti, “Kodi ati iwe ndiwe mfulu yachiroma?” Iye adati, “Inde.” Tsono mkulu uja adamuuza kuti, “Ine ndidachita chogula ufulu wangawu ndi ndalama zambiri.” Paulo adati, “Koma ine wangawu ndidachita chobadwa nawo.” Pompo asilikali aja amene adaati afunse Paulo mafunso, adamleka. Mkulu ujanso adachita mantha atazindikira kuti adaamanga munthu amene ali mfulu yachiroma. Mkulu wa asilikali uja adaafuna kudziŵa kwenikweni chifukwa chimene Ayuda adaadzanenezera Paulo. Choncho m'maŵa mwake adammasula, nalamula kuti akulu a ansembe ndi onse a pa Bwalo Lalikulu lamilandu la Ayuda asonkhane. Kenaka adabwera ndi Paulo namuimika pakati pao. Paulo adaŵapenyetsetsa a m'Bwalo Lalikulu aja nati, “Abale anga, ine moyo wanga wonse mpaka lero lino ndakhala ndi mtima wangwiro pamaso pa Mulungu.” Apo Ananiya, mkulu wa ansembe onse, adalamula amene adaaimirira pafupi ndi Paulo kuti, “Mtchayeni kukamwako!” Pamenepo Paulo adamuuza kuti, “Mulungu adzatchaya iweyo, chipupa chopaka njeresawe! Iwe wakhala pamenepo kuti undiweruze potsata Malamulo a Mose, nanga bwanji ukuŵaphwanya Malamulowo pakulamula kuti anditchaye?” Apo amene adaaimirira pafupi adauza Paulo kuti, “Bwanji ukunena zachipongwe kwa mkulu wa ansembe wa Mulungu?” Paulo adati, “Pepani abale, sindimadziŵa kuti ndi mkulu wa ansembe onse. Paja mau a Mulungu akuti, ‘Usamnenere zoipa woweruza anthu ako.’ ” Pamene Paulo adaona kuti ena mwa iwo ndi a m'gulu la Asaduki, ena a m'gulu la Afarisi, adanena mokweza mau m'Bwalo muja kuti, “Abale anga, inetu ndine Mfarisi, mwana wa Mfarisi. Ineyo ndikuweruzidwa chifukwa ndimakhulupirira kuti anthu adzauka kwa akufa.” Atanena zimenezi, Afarisi ndi Asaduki aja adayamba kukangana, ndipo msonkhano udagaŵana. Paja Asaduki amati anthu sadzauka kwa akufa, ndiponso kuti kulibe angelo kapena mizimu. Koma Afarisi amakhulupirira zonsezi. Anthu aja adayamba kufuula kwambiri. Tsono aphunzitsi ena a Malamulo, a m'gulu la Afarisi, adaimirira nanenetsa kuti, “Sitikupeza konse cholakwa mwa munthuyu ai. Mwina nkukhala kuti mzimu kapena mngelo walankhula naye!” Anthu aja adafika pokangana koopsa, kotero kuti mkulu wa asilikali uja ankaopa kuti angamkadzule Paulo. Choncho adalamula asilikali kuti, “Pitani mukamlanditse kwa anthuwo, mukamloŵetse m'linga la asilikali.” Tsiku lomwelo, usiku, Ambuye adadzaima pafupi ndi Paulo namuuza kuti, “Limba mtima. Monga wandichitira umboni kuno ku Yerusalemu, uyenera kukandichitiranso umboni ku Roma.” Kutacha, Ayuda ena adakhala upo, ndipo adapangana molumbira kuti, “Ife sitidya kapena kumwa chilichonse mpaka titamupha Pauloyo basi.” Anthu amene adaapangana za chiwembu chimenechi analipo opititira makumi anai. Iwowo adapita kwa akulu a ansembe ndi kwa akulu a Ayuda nakaŵauza kuti, “Ife talumbira kolimba kuti sitilaŵa kanthu mpaka titamupha Pauloyu. Tsono inu, pamodzi ndi Bwalo Lalikulu lamilandu, mutumize mau kwa mkulu wa asilikali kuti abwere naye Paulo kwa inu, ngati kuti mukufuna kufunsitsa bwino za mlandu wake. Ife tili okonzeka kudzamuphha asanafike kuno.” Koma mwana wa mlongo wake wa Paulo atamva za chiwembuchi, adakaloŵa m'linga la asilikali lija nakamtsina khutu Paulo. Apo Paulo adaitana mmodzi mwa atsogoleri a asilikali namuuza kuti, “Tapitani ndi mnyamatayu kwa mkulu wa asilikali, akuti ali naye ndi mau.” Iye adamtengadi mnyamatayo kupita naye kwa mkulu wa asilikali, namuuza kuti, “Mkaidi uja Paulo anandiitana, nandipempha kuti ndibwere ndi mnyamatayu kwa inu, akuti ali nanu ndi mau.” Mkulu wa asilikali uja adamgwira pa dzanja mnyamatayo, namtengera pambali, ndipo ali paokha adamufunsa kuti, “Kodi ndi mau anji ukufuna kundiwuza?” Iyeyo adati, “Ayuda ena apangana zodzakupemphani kuti mupite ndi Paulo ku Bwalo lao Lalikulu lamilandu maŵa, ngati kuti iwowo akufuna kufunsitsa bwino za mlandu wake. Koma pepani, inu musaŵamvere, chifukwa pali anthu opitirira makumi anai amene akukamlalira Paulo pa njira. Iwowo alumbira kuti sadzadya kapena kumwa chilichonse mpaka atamupha. Panopa ali okonzeka ndipo akungodikira kuti inu muŵabvomere.” Tsono mkulu wa asilikali uja adauza mnyamatayo kuti, “Chabwino, iwe pita, koma usaululire wina aliyense kuti wadzandifotokozera zimenezi.” Mkulu wa asilikali uja adaitana atsogoleri aŵiri a asilikali naŵauza kuti, “Uzani asilikali 200 akhale okonzeka kuyambira nthaŵi ya 9 koloko usiku uno, kupita ku Kesareya pamodzi ndi asilikali makumi asanu ndi aŵiri okwera pa kavalo, ndiponso 200 amikondo. Mumkonzerenso Paulo akavalo kuti akwerepo, ndipo mukamufikitse bwino kwa Felikisi, bwanamkubwa.” Tsono adalemba kalata iyi: “Ine Klaudio Lisiasi, ndikupereka moni kwa inu olemekezeka, a Felikisi, bwanamkubwa. Munthuyo Ayuda adaamugwira, ndipo anali pafupi kumupha. Nditamva kuti iyeyo ndi mfulu wachiroma, ndidapita ndi asilikali nkukamlanditsa. Ndinkafuna kudziŵa chifukwa chimene ankamunenezera, choncho ndidapita naye ku Bwalo lao Lalikulu lamilandu. Ndidapeza kuti ankamneneza chifukwa cha nkhani yokhudza Malamulo ao, koma osati mlandu womuphera kapena womuponyera m'ndende. Tsono popeza kuti ndamva kuti pali chiwembu chimene ampanganirana munthuyu, ndamtumiza kwa inu msanga. Ndauza omnenezawo kuti adzanene mau ao kwa inu.” Pamenepo asilikali aja adatenga Paulo monga momwe adaaŵalamulira, napita naye ku Antipatri usiku. M'maŵa mwake iwo adabwerera ku linga la asilikali, nasiya okwera pa kavalo aja kuti apitirire ndi Paulo. Iwo aja atafika ku Kesareya, adapereka kalata ija kwa bwanamkubwa, naperekanso Paulo m'manja mwake. Bwanamkubwa uja ataŵerenga kalatayo, adafunsa Paulo za dera kumene ankachokera. Pamene adamva kuti ngwochokera ku Silisiya, adamuuza kuti, “Ndidzamva mlandu wako akadzabwera okunenezawo.” Atatero adalamula kuti abamulondera ku nyumba ya mfumu Herode. Patapita masiku asanu, Ananiya, mkulu wa ansembe onse, adadza pamodzi ndi akuluakulu ena a Ayuda, ndi katswiri wina wolankhulira anthu pa milandu, dzina lake Tertulo. Iwo adafika pamaso pa bwanamkubwa uja, nayamba kuneneza Paulo. Tsono Pauloyo atamuitana, Tertulo uja adayambapo zomunenezazo. Adati, “Inu a Felikisi olemekezeka, ife tikukhala pa mtendere weniweni chifukwa cha inu, ndipo zinthu zambiri zakhala zikukonzeka m'dziko mwathu chifukwa cha utsogoleri wanu wanzeru. Zonsezi timazilandira moyamika kwambiri ponseponse mwa njira iliyonse. Pepani sindikufuna kukutayitsani nthaŵi, komabe ndimapempha kuti mundikomere mtima, mungomvapo mau athuŵa mwachidule. Ndiye kuti munthu uyu ife tampeza kuti ngwovutitsa kwabasi. Wakhala akuutsa chipolowe pakati pa Ayuda pa dziko lonse lapansi, ndiponso ndi mtsogoleri wa gulu lopatulika la Anazarete. Adaayesanso ngakhale kuipitsa Nyumba ya Mulungu yathu. Ndiye ife tidamgwira.” [“Tidafuna kumuweruza potsata Malamulo athu. Koma Lisiasi, mkulu wa asilikali, adadzamtsomphola kumanja kwathu mwankhondo, kenaka nkulamula kuti omneneza adzaonekere kwa inu.”] “Mukamufunsa ameneyu, mutha kudziŵa nokha zonse zimene tikumnenezera.” Ayudanso adavomereza, nanenetsa kuti zonsezo nzoona. Bwanamkubwa uja adakodola Paulo kuti alankhule, ndipo Paulo adati, “Ndikudziŵa kuti inu mwakhala mukuweruza mtundu uwu zaka zambiri tsopano, nchifukwa chake ndakondwa kuti ndiyankhe pamaso panu zimene akundinenezazi. Inu nomwe mutha kupeza umboni wake, sipadapite masiku opitirira khumi ndi aŵiri chipitire changa ku Yerusalemu kukapembedza. Ayuda sadandipezepo ndikukangana ndi munthu aliyense m'Nyumba ya Mulungu, kapena kuutsa chipolowe pakati pa anthu m'nyumba zamapemphero, kaya pena paliponse mumzindamo. Iwoŵa sangakutsimikizireni zimene akundinenezazi. Koma ichi chokha ndikuvomera pamaso panu, kuti ndimapembedza Mulungu wa makolo athu potsata Njira imene iwoŵa amati ndi gulu lopatulika. Ndimakhulupirira zonse zolembedwa m'Malamulo a Mose ndiponso m'mabuku a aneneri. Popeza kuti ndimakhulupirira Mulungu, ndimakhulupirira, monga iwonso amakhulupirira, kuti anthu onse, olungama ndi osalungama omwe, adzauka kwa akufa. Nchifukwa chake inenso ndimayesetsa nthaŵi zonse kukhala ndi mtima wangwiro pamaso pa Mulungu, ndi pamaso pa anthu. “Tsono nditakhala kwina zaka zingapo, ndidabwera kudzatula zopereka zachifundo kwa anthu a mtundu wanga, ndiponso kudzapereka nsembe. Pamene ndinkachita zimenezi, iwo adandipeza m'Nyumba ya Mulungu nditachita mwambo wakudziyeretsa. Panalibe konse khamu la anthu kapena chipolowe ai. Koma kunali Ayuda ena a ku Asiya. Iwowo akadayenera kukhala pano pamaso panu kudzandineneza okha ngati ali nane nkanthu. Kapena omwe ali panoŵa anene ngati adandipeza cholakwa pamene ndinali m'Bwalo lao Lalikulu lamilandu. Koma cholakwa changa chingathe kukhala chokhachi chakuti, pamene ndidaaimirira pamaso pao, ndidaafuula kuti, ‘Mukundizenga mlandu ine lero chifukwa ndimakhulupirira kuti anthu akufa adzauka.’ ” Felikisi ankadziŵa bwino za Njira ya Ambuye, choncho adatseka bwalolo ndi mau akuti, “Ndidzagamula mlandu wako akabwera Lisiasi, mkulu wa asilikali.” Tsono adalamula mtsogoleri wa gulu la asilikali kuti azimlonda, koma azimpatsakonso ufulu, osaletsa abwenzi ake kumamsamala. Patapita masiku angapo Felikisi adabwera ndi mkazi wake Durusila, amene anali Myuda. Adaitana Paulo, nayamba kumvetsera zimene iye ankalankhula za kukhulupirira Khristu Yesu. Koma pamene Paulo adakamba za chilungamo, za kudziletsa, ndi zakuti Mulungu adzaweruza anthu, Felikisi adachita mantha namuuza kuti, “Pakali pano bapita, ndikapeza nthaŵi, ndichita kukuitananso.” Koma ankaganiza kuti Paulo adzampatsa ndalama, nchifukwa chake ankamuitana kaŵirikaŵiri namacheza naye. Patapita zaka ziŵiri, Porkio Fesito adaloŵa m'malo mwa Felikisi. Tsono Felikisiyo pofuna kuchita mkomya kwa Ayuda, adamsiya m'ndende Paulo uja. Fesito adayamba ntchito yoweruza m'chigawo chake, ndipo patapita masiku atatu, adapita ku Yerusalemu kuchokera ku Kesareya. Kumeneko akulu a ansembe ndiponso atsogoleri a Ayuda adamufotokozera za mlandu wa Paulo. Iwo adapempha Fesito kuti aŵakomere mtima pakumtumiza Paulo ku Yerusalemu. Adaatero chifukwa anali atapangana zomulalira Paulo kuti amuphe pa njira. Fesito adaŵauza kuti, “Paulo akusungidwa m'ndende ku Kesareya, ndipo ine ndipita komweko posachedwa. Tsono atsogoleri anu apite nane pamodzi kumeneko, kuti akamneneze munthuyo ngatidi iye adachitapo cholakwa.” Fesito atakhala pakati pao ku Yerusalemu kuja masiku osapitirira asanu ndi atatu kapena khumi, adapita ku Kesareya. M'maŵa mwake adakhala pa mpando woweruzira milandu, naitanitsa Paulo kuti abwere pamaso pake. Paulo atafika, Ayuda amene adaabwera kuchokera ku Yerusalemu aja adamzinga, nayamba kumneneza zinthu zoopsa zambiri, zimene iwo sadathe kuzitsimikiza. Paulo poyankha zomnenezazo adati, “Ine sindidalakwirepo Malamulo a Ayuda, kapena Nyumba ya Mulungu, kapenanso Mfumu ya ku Roma.” Fesito pofuna kuchita mkomya kwa Ayuda, adafunsa Paulo kuti, “Kodi ungakonde kupita ku Yerusalemu kuti mlandu wakowu ukazengedwere kumeneko pamaso panga?” Koma Paulo adati, “Ine ndaima pa bwalo lamilandu la Mfumu ya ku Roma, ndiko kumene ayenera kundiweruza. Ayudaŵa ine sindidaŵalakwire chilichonse, monga inu mukudziŵa bwino. Ngati ndili wolakwa, ndipo ngati ndachita kanthu koyenera kuti ndiphedwe, sindikukana kuphedwa ai. Koma ngati zimene aŵa akundinenezazi si zoona, palibe munthu angathe kundipereka kwa iwo. Ine ndikupempha kuti mlandu wangawu ndikagwade kwa Mfumu ya ku Roma.” Tsono Fesito atakambirana ndi abwalo ake, adati, “Wachita apilo kwa Mfumu ya ku Roma. Chabwino, udzapitadi ku Romako kwa Mfumu yaikulu.” Patapita masiku, mfumu Agripa pamodzi ndi mkazi wake Berenise adadza ku Kesareya kudzalonjera Fesito. Atakhala kumeneko masiku angapo, Fesitoyo adafotokozera mfumoyo za mlandu wa Paulo. Adati, “Kuli munthu wina kuno amene Felikisi adamsiya m'ndende. Pamene ndinali ku Yerusalemu, akulu a ansembe pamodzi ndi atsogoleri a Ayuda adandifotokozera za iye, nandipempha kuti ndizenge mlandu wake ndi kugamula kuti ngwolakwa. Ine ndidaŵayankha kuti si mwambo wa Aroma kungompereka munthu ai. Munthu wonenezedwayo amayamba wakumana nawo omnenezawo, kuti iyeyo akhale ndi mwai woyankhapo pa zimene akumnenezazo. Tsono iwo atadzasonkhana kuno, ineyo mosataya nthaŵi, m'maŵa mwake ndidakakhala pa mpando woweruzira milandu, nkumuitanitsa munthuyo kuti abwere pamaso panga. Omneneza aja ataimirira, sadamneneze choipa nchimodzi chomwe pa zimene ndinkaganiza ine. Ankangokangana naye za chipembedzo chao, ndiponso ati za munthu wina dzina lake Yesu, amene adafa, koma Paulo amatsimikiza kuti ali moyo. Ine ndidaathedwa nzeru, osadziŵa kuti ndiifufuze bwanji nkhani imeneyi. Choncho ndidamufunsa Pauloyo ngati akadakonda kupita ku Yerusalemu kuti mlandu wakewo ukazengedwere kumeneko. Koma Paulo adapempha kuti abasungidwa m'ndende mpaka Mfumu ya ku Roma itatsimikiza za mlandu wake. Pamenepo ndidalamula kuti amsunge m'ndende kufikira nditamtumiza kwa Mfumuyo.” Apo Agripa adauza Fesito kuti, “Inenso nkadakonda kuti ndidzimvere ndekha zimene munthuyu anene.” Fesito adati, “Mumumva maŵa.” M'maŵa mwake Agripa ndi Berenise adabwera ndi ulemu waukulu wachifumu. Adaloŵa m'bwalo la milandu pamodzi ndi akulu a asilikali ndiponso akuluakulu a mumzindamo. Fesito adaitanitsa Paulo kuti abwere, iye nkubweradi. Tsono Fesito adati, “Mfumu Agripa, ndi inu nonse amene muli nafe muno, mukumuwona munthu uyu. Ayuda onse adandipempha ku Yerusalemu ndi kuno komwe mofuula kuti ameneyu sayenera kukhalanso moyo. Koma ine sindidapeze konse kuti iye adachita kanthu koyenera kumuphera. Ndiye popeza kuti mwiniwakeyu adapempha kuti mlandu wake ukazengedwe ndi Mfumu ya ku Roma, ndidatsimikiza zomtumiza. Komabe ndilibe kanthu kenikeni koti ndilembere mfumuyo za iyeyu. Motero ndabwera naye kwa inu, makamaka kwa inuinuyo mfumu Agripa, kuti mutamufunsitsa, ndikhale nkanthu koti ndilembe. Ine ndiye ndikuwona kuti ndi chinthu chopusa kutumiza mkaidi popanda kutchula zifukwa za mlandu wake.” Agripa adauza Paulo kuti, “Tikukulola kuti unene mau ako.” Tsono Paulo adatambalitsa dzanja lake nayamba kunena nkhani yake. Adati, “Inu Mfumu Agripa, ine ndikuganiza kuti ndine wamwai kuti ndi pamaso panu pamene ndiyankhe lero zonse zimene Ayuda akhala akundineneza. Makamaka chifukwa inu mumaidziŵa bwino miyambo yonse yachiyuda, ndiponso mikangano yao yonse, ndikukupemphani kuti mundimvere moleza mtima. “Ayuda onse akudziŵa za moyo wanga wonse kuyambira ndili mwana. Akudziŵa m'mene ndinkakhalira chiyambire pakati pa anthu a mtundu wanga, ndiponso ku Yerusalemu. Iwo adandidziŵa kuyambira kale, ndipo ngati afuna, angathe kundichitira umboni kuti moyo wanga wonse ndakhala Mfarisi, mmodzi wa gulu lija limene limasamala chipembedzo chathu koposa. Ndipo tsopano ngati akundizenga mlandu, nchifukwa chakuti ndikuyembekeza zimene Mulungu adalonjeza makolo athu. Mafuko onse khumi ndi aŵiri a mtundu wathu, popembedza Mulungu usana ndi usiku mosafookera, amayembekeza kudzalandira zimene Iye adalonjezazo. Mwakuti nchifukwa cha chiyembekezo chimenechi, amfumu, kuti Ayuda akundineneza. Bwanji ena mwa inu Ayuda mumayesa kuti nkosatheka kukhulupirira kuti Mulungu nkuukitsa anthu kwa akufa? “Ine ndemwe ndinkaganiza kuti ndinkayenera kuchita zinthu zambiri pofuna kuthetsa mbiri ya Yesu wa ku Nazarete. Ndipo ndidaazichitadi ku Yerusalemu. Akulu a ansembe atandipatsa ulamuliro, ine ndinkaŵatsekera m'ndende anthu ambiri a Mulungu. Pamene iwo ankaphedwa, ine ndinkavomereza. Kaŵirikaŵiri ndinkaŵalanga m'nyumba zonse zamapemphero, ndi kuyesa kuŵakakamiza kuti amnyoze Yesuyo. Ndinkaŵachitira ukali woopsa, kotero kuti ndinkaŵazunza ngakhale ku mizinda ya ku maiko achilendo.” “Pa ulendo wina wotere, ndinkapita ku Damasiko ndi ulamuliro ndi mphamvu zondipatsa akulu a ansembe. Pa njira, nthaŵi yamasana dzuŵa lili pa mutu, inu amfumu, ndidaona kuŵala kochokera kumwamba. Kuŵalako kunali koposa kuŵala kwa dzuŵa, ndipo kudatizinga tonse, ine ndi anzanga aulendo. Tonse tidagwa pansi, ndipo ine ndidamva mau ondiwuza pa Chiyuda kuti, ‘Saulo, Saulo, ukundizunziranji? Ukungodzipweteka wekha ngati ng'ombe yoponda zidyali pa chobayira.’ Apo ndidafunsa kuti, ‘Ndinu yani, Ambuye?’ Ambuyewo adati, ‘Ine ndiye Yesu, amene ukumzunza. Koma dzuka, imirira. Pakuti ndakuwonekera kuti ndikuike kuti ukhale mtumiki wanga ndi mboni yanga. Ndifuna kuti ukhale mboni ya m'mene wandiwonera lero, ndiponso ya zimene ndidzakuwonetsa m'tsogolo. Ndidzakulanditsa kwa anthu a mtundu wako, ndiponso kwa anthu a mitundu ina kumene ndikukutuma. Ndikukutuma kuti anthu ameneŵa uŵatsekule maso, kuti atembenuke kuchoka mu mdima wa machimo nkuloŵa m'kuŵala, ndiponso kuchoka m'mphamvu ya Satana nkutsata Mulungu. Ndifuna kuti akhulupirire Ine, kuti machimo ao akhululukidwe, ndipo alandire nao madalitso pamodzi ndi anthu amene Mulungu adaŵasankha kuti akhale akeake.’ “Nchifukwa chake, mfumu Agripa, sindidakane kumvera zimene Mulungu adandiwonetsa m'masomphenyazo. Koma ndidalalika poyamba kwa anthu a ku Damasiko ndi a ku Yerusalemu, ndipo bwino lake ku dziko lonse la Yudeya, ndiponso kwa anthu a mitundu ina. Ndidalalika kuti atembenuke mtima, kutembenukira kwa Mulungu, ndi kuchita ntchito zotsimikiza kuti atembenukadi mtima. Chifukwa cha zimenezi Ayuda adandigwira m'Nyumba ya Mulungu nafuna kundipha. Koma Mulungu wakhala akundithandiza mpaka lero. Motero ndaimirira pano kuti ndichite umboni pamaso pa anthu onse, aakulu ndi ang'ono omwe. Zimene ndikuŵauza si zina ai, koma ndi zomwezo zimene aneneri ndi Mose adanena kuti zidzachitika. Paja iwo adati Mpulumutsi wolonjezedwa uja adzamva zoŵaŵa, ndipo popeza kuti Iye adzakhala woyamba kuuka kwa akufa, adzalengeza Ayuda ndi amene sali Ayuda za kuŵala kwa chipulumutso.” Pamene Paulo ankadziteteza ku zomnenezazo, Fesito adanena mokweza mau kuti, “Misalatu imeneyi, iwe Paulo! Kuphunziritsa kwako kukukupengetsa.” Koma Paulo adati, “Pepani, a Fesito olemekezeka, sindine wamisala ai. Zimene ndikunenazi nzoona ndi zanzeru. Mfumu Agripa akudziŵa zonsezi, nkuwona ndikulankhula pamaso pao momasuka. Ndikhulupirira kuti palibe kanthu nkamodzi komwe pa zimenezi kamene iwo sakadziŵa. Pakuti sizidachitike mobisika ai. Inu mfumu Agripa, kodi mumakhulupirira mau a aneneri? Ndikudziŵa kuti mumaŵakhulupirira.” Apo Agripa adauza Paulo kuti, “Uganiza kuti nkundisandutsa mkhristu pa kanthaŵi kochepa, komweka?” Paulo adati, “Kaya ndi pa kanthaŵi kochepa kaya nthaŵi yaitali, Mulungu akadalola kuti osati inu nokha, komanso anthu onse amene alikumva mau anga lero, akhale monga momwe ndiliri inemu, kupatula maunyolo okhaŵa.” Pamenepo mfumu Agripa, bwanamkubwa, Berenise, ndi onse amene anali nawo adaimirira. Atachokapo adauzana kuti, “Munthuyu sakuchita chilichonse choyenera kumuphera kapena kumponyera m'ndende.” Tsono Agripa adauza Fesito kuti, “Tikadammasula munthuyu akadapanda kupempha kuti mlandu wakewu ukazengedwe ndi Mfumu ya ku Roma.” Zitatsimikizika kuti tiyenera kupita ku Italiya pa chombo, adampereka Paulo pamodzi ndi akaidi ena kwa mtsogoleri wa asilikali, dzina lake Julio, wa gulu la asilikali lochedwa gulu la Augusto. Tidakwera chombo chochokera ku Adramitio chimene chinali chokonzeka kale kupita ku madooko a ku Asiya, ndipo tidanyamuka. Aristariko, Mmasedoni wa ku mzinda wa Tesalonika, anali nafe. M'maŵa mwake tidafika ku Sidoni, ndipo Julio adakomera mtima Paulo, namlola kupita kwa abwenzi ake kuti akamsamale. Kuchokera kumeneko tidadzera kumpoto kwa chilumba cha Kipro chifukwa mphepo inkawomba mopenyana nafe. Tidawoloka nyanja mbali ya ku Silisiya ndi Pamfiliya nkumafika ku Mira, mzinda wa ku Likiya. Kumeneko mtsogoleri wa asilikali uja adapezako chombo chochokera ku Aleksandriya chimene chinkapita ku Italiya, ndipo adatikweza m'chombo chimenechi. Tidayenda pang'onopang'ono pa masiku angapo, nkukafika pafupi ndi Kinido movutikira. Tsono popeza kuti mphepo idaativuta zedi, tidalephera kupitirira ulendo wathu molunjika, choncho tidadzera kumwera kwa chilumba cha Krete, titabzola Salimone. Tidayenda movutikira m'mbali mwa chilumbacho, nkukafika ku malo ena otchedwa Madooko Okoma, pafupi ndi mzinda wa Lasea. Nthaŵi yaikulu idapita, ndipo ngakhale nthaŵi yosala zakudya inali itapita kale. Nthaŵiyo ulendo wapamadzi unali woopsa. Pamenepo Paulo adaŵachenjeza kuti, “Abale, ine ndikuwona kuti pa ulendowu zinthu zambiri zidzawonongeka ndi kutayika, osati katundu yekha ndi chombo ai, komanso moyo wathu.” Koma mtsogoleri wa asilikali uja adamvera kapitao wa chombo ndiponso mwiniwake wa chombocho, osati mau a Paulo ai. Tsono popeza kuti dooko silinali labwino kukhalako pa nthaŵi yachisanu, ambiri mwa iwo adafuna kuchokako, nayesa kuti angathe kukafika ku Fenikisi nkukakhala kumeneko pa nthaŵi yachisanu. Fenikisi linali dooko la ku Krete, loloza kumwera chakumadzulo, ndiponso kumpoto chakumadzulo. Mphepo yakumwera itayamba kuwomba monyengerera, anthu aja adayesa kuti tsopano apeza mpata woti achite zimene ankafuna. Motero adanyamuka ulendo, nayenda m'mbali mwa chilumba chija cha Krete. Koma posachedwa mphepo yamkuntho, yotchedwa Yurakulo, idayamba kuwomba kuchokera ku mtunda. Idaomba chombo chija, ndiye popeza kuti sitidathe kuchiwongolera moyang'anana ndi mphepoyo, tidaigonjera nkungotengedwa nayo. Tidafika pafupi ndi kachilumba kotchedwa Kauda, ku mbali yosawombapo mphepo. Kumeneko movutikira tidatha kuwongolera kabwato kokokedwa ndi chombo chija. Kenaka adakweza kabwatoko pa chombo, ndipo pambuyo pake adakulunga chombocho ndi zingwe kuti achilimbitse. Tsono poopa kuti angakagunde ku mchenga wa ku Siriti, adatsitsa mathanga nalola kungotengedwa ndi mphepo. Popeza kuti tinkavutika naye kwambiri namondweyo, m'maŵa mwake adayamba kutaya katundu m'madzi. Ndipo pa tsiku lachitatu lake adataya m'nyanja ndi zipangizo za chombo zomwe. Sitidaone dzuŵa kapena nyenyezi masiku ambiri, koma namondwe ankakalipabe, mpaka tonse tidaatayiratu chikhulupiriro chakuti tipulumuka. Pa nthaŵi yaitali anthu aja sadadye kanthu. Tsono Paulo adaimirira pakati pao nati, “Abale, mukadamvera zija ndidaanena inezi, osachoka ku Krete, sibwenzi zinthu zitawonongeka nkutayika chotere. Koma tsopano ndikukuuzani kuti mulimbe mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe mwa inu amene atayike, koma chombo chokha ndiye chiwonongeke. Usiku womwe wathawu kunandibwerera mngelo wa Mulungu, Mulungu amene ine ndili wake, ndipo amene ndimamlemekeza. Mngeloyo anandiwuza kuti, ‘Usachite mantha, Paulo. Uyenera kukaima pamaso pa Mfumu ya ku Roma. Mulungu, mwa kukoma mtima kwake, walola kuti anzako onse aulendo akhale moyo.’ Ndiye inu, limbani mtima, pakuti ndikukhulupirira Mulungu, kuti zimene wandiwuzazi zidzachitikadi momwemo. Koma tidzatsakamira pa chilumba china.” Pakati pa usiku wa khumi ndi chinai, mphepo ikutikankhabe pa nyanja ya Adriya, antchito apachombo adaganiza kuti akuyandikira mtunda. Tsono atayesa kuzama kwa nyanja, adapeza mamita 37. Atayenda pang'ono, adayesanso napeza mamita 27. Poopa kuti chombo chingakatsakamire pa matanthwe, adatsitsira anangula anai m'nyanja kumbuyo kwa chombo. Kenaka ankangoyembekeza molakalaka kuti kuche. Antchito apachombo aja ankafuna kuthaŵamo m'chombo muja. Choncho adatsitsira kabwato kaja pa madzi, nachita ngati akufuna kutsitsira anangula m'nyanja kutsogolo kwa chombo. Apo Paulo adauza mtsogoleri wa asilikali uja, pamodzi ndi asilikali ake omwe kuti, “Ngati anthu aŵa sakhala m'chombo muno, ndithu inu simutha kupulumuka ai.” Pamenepo asilikali aja adadula zingwe za kabwato kaja nakaleka kuti kagwe. Kuli pafupi kucha, Paulo adaŵapempha onse aja kuti adyeko kanthu. Adaŵauza kuti, “Mwakhala masiku khumi ndi anai tsopano mitima ili m'malere, nthaŵi yonseyi osadya kapena kulaŵa kanthu. Ndikukupemphani tsono mudye kanthu kuti mupulumuke. Palibe ndi mmodzi yemwe mwa inu amene adzataye ngakhale tsitsi limodzi la kumutu kwake.” Atanena zimenezi, Paulo adatenga buledi, nayamika Mulungu pamaso pa onse. Ndipo adamnyema bulediyo nayamba kudya. Pamenepo onse aja adalimba mtima, iwonso nkuyamba kudya. Tonse pamodzi tinali anthu okwanira 276 m'chombomo. Onse aja atadya nkukhuta, adapeputsa chombo pakutaya tirigu m'nyanja. Kutacha, anthu sadazindikire mtundawo, koma adaona bondo la nyanja lamchenga. Tsono adaganiza kuti ngati nkotheka, akakocheze chombo kumeneko. Choncho adataya anangula naŵasiya m'nyanja. Nthaŵi yomweyo adamasula zingwe zomangira nkhafi zoongolera, nakweza thanga lakutsogolo, kuti mphepo ikankhe chombo, ndipo adalunjika ku mtunda. Koma chombo chija chidakatsakamira pa mchenga wobisika ndi madzi, ndipo chidaima. Mbali yakutsogolo ya chombocho idajima, kotero kuti sichidathe kuyendanso. Ndipo mbali yakumbuyo idaonongeka ndi mphamvu ya mafunde. Asilikali aja adaganiza zakupha akaidi, kuwopa kuti ena mwa iwo angasambire kukafika ku mtunda nkuthaŵa. Koma mtsogoleri wa asilikali uja adafuna kupulumutsa Paulo, motero adaŵaletsa. Adalamula kuti onse otha kusambira, adziponye m'madzi, asambire kuti akafike ku mtunda. Otsalawo adaŵalamula kuti agwire matabwa kapena zina za chombo choswekacho. Motero onse adapulumuka nakafika kumtunda. Titapulumuka choncho, tidamva kuti chilumbacho dzina lake ndi Melita. Anthu apamenepo adatichitira zabwino kwambiri. Adatilandira bwino natisonkhera moto, chifukwa kudaayamba kugwa mvula ndipo kunkazizira. Paulo adakatola nkhuni nabwerako ndi mtolo, ndipo pamene ankaziika pa moto, mumtolomo mudatuluka mphiri chifukwa cha kutenthako. Idamluma nkukanirira ku dzanja lakelo. Pamene anthuwo adaona njokayo ili lende ku dzanja lake, adayamba kuuzana kuti, “Ndithudi munthu ameneyu nchigaŵenga. Ngakhale wapulumuka pa nyanja, koma Mulungu wachilungamo sadamlole kuti akhale ndi moyo.” Komabe Paulo adaikutumulira pa moto njokayo, osapwetekedwa konse. Anthu aja ankayembekeza kuti thupi lake litupa, kapena kuti agwa mwadzidzidzi nkufa. Adakhala akumuyang'ana nthaŵi yaitali, koma ataona kuti palibe chilichonse chachilendo chimene chamchitikira, adasintha maganizo nati, “Ameneyu ndi mmodzi wa milungu.” Pafupi ndi malowo panali minda ya Publio, mkulu wa pachilumbapo. Iye adatilandira natisamala bwino masiku atatu. Bambo wake wa Publioyo anali gone, chifukwa ankadwala malungo ndi kamwazi. Paulo adaloŵa m'chipinda chake nayamba kupemphera, ndipo adamsanjika manja nkumuchiritsa. Zitachitika zimenezi, anthu ena onse odwala pachilumbapo adabwera, Paulo nkuŵachiritsa. Anthu aja adatipatsa mphatso zambiri, ndipo pamene tidanyamukanso ulendo wathu wapachombo, adatipatsa zonse zosoŵeka. Patapita miyezi itatu, tidanyamukadi ulendo wathu pa chombo china, chimene chidaakhala pachilumbapo pa nthaŵi yachisanu. Chombocho chinali chochokera ku Aleksandriya, ndipo chinkatchedwa “Ana Amapasa.” Titafika ku Sirakusa, tidakhalako masiku atatu. Kuchokera kumeneko tidapitirira nkukafika ku Regio. Patapita tsiku limodzi, mphepo ya mwera idayamba kuwomba, choncho pa tsiku lotsatira tidafika ku Puteoli. Kumeneko tidapeza abale, ndipo adatiitana kuti tikhale nawo masiku asanu ndi aŵiri. Motero tidakafika ku Roma. Abale akumeneko atamva za ife, adabwera mpaka ku Bwalo la Apio ndiponso ku Nyumba za Alendo Zitatu kudzatichingamira. Paulo ataona ataŵaona, adayamika Mulungu, nalimba mtima. Pamene tidaloŵa mu mzinda wa Roma, Paulo adaloledwa kukhala kwayekha ndi msilikali womulonda. Patapita masiku atatu, Paulo adasonkhanitsa atsogoleri a Ayuda akomweko. Atasonkhana, iye adaŵauza kuti, “Abale anga, ine ndili kuno ngati mkaidi wochokera ku Yerusalemu. Ngakhale sindidalikwire mtundu wathu, kapena miyambo ya makolo athu, komabe ndidaperekedwa kwa Aroma. Iwo atandifunsa, adaafuna kundimasula, chifukwa sadapeze mlandu woyenera kundiphera. Koma pamene Ayuda adakana, ndidakakamizidwa kupempha kuti mlandu wangawo ndidzagwade kwa Mfumu ya ku Roma kuno. Sikuti ndinali ndi kanthu konenezera mtundu wanga ai. Nkuwona ndakuitanani kuti ndilankhule nanu. Pakuti ndamangidwa ndi unyolo uwu chifukwa chokhulupirira chinthu chimene Aisraele akuyembekeza.” Atsogoleriwo adamuyankha kuti, “Ife sitidalandirepo makalata ochokera ku Yudeya onena za inu. Palibenso wina mwa abale athu amene adafika kuno kudzatifotokozera kapena kudzatiwuza zoipa za inu. Koma makamaka nkwabwino kuti mutiwuze maganizo anu, pakuti za gulu lanu lopatulikali tikudziŵa kuti ponseponse anthu akutsutsana nalo.” Pamenepo iwo adapangana naye tsiku, ndipo ambiri adaabwera kunyumba kumene iye ankakhala. Kuyambira m'maŵa mpaka madzulo Paulo adakhala akulankhula nawo, naŵafotokozera za ufumu wa Mulungu. Pakuŵatchulira mau a m'Malamulo a Mose ndiponso m'mabuku a aneneri, ankayesa kuŵakopa kuti akhulupirire Yesu. Ena adakopekadi ndi zimene iye adanena, koma ena sadakhulupirire. Tsono popeza kuti anthuwo sadamvane, adangochokapo. Komabe asanachoke, Paulo adaawonjezapo mau amodzi aŵa akuti, “Mzimu Woyera adaanena zoona pamene adaauza makolo anu mwa mneneri Yesaya kuti, “ ‘Pita kwa anthu a mtundu uwu ndi kuŵauza kuti: Kumva mudzamva, koma osamvetsa, kupenya mudzapenya, koma osazindikira. Ndithu mtima wa anthu a mtundu uwu wauma, agonthetsa makutu ao ndipo atseka maso ao, kuwopa kuti angaone ndi maso ao, ndipo angamve ndi makutu ao, angamvetse ndi mtima wao, natembenukira mwa Ine kuti ndiŵachitiritse.’ ” Paulo adaŵauza kuti, “Dziŵani tsono kuti Mulungu watumiza chipulumutso chakechi kwa anthu a mitundu ina. Iwowo adzamva.” [ Paulo atanena mau ameneŵa, Ayuda aja adachokapo akutsutsana kwambiri.] Tsono Paulo adakhala kumeneko zaka ziŵiri zathunthu m'nyumba yake yobwereka, ndipo ankaŵalandira bwino lomwe onse obwera kudzamuwona. Ankalalika za ufumu wa Mulungu, ndi kumaphunzitsa za Ambuye Yesu Khristu poyera, popanda wina aliyense womuletsa. Ndine, Paulo, mtumiki wa Yesu Khristu. Mulungu adandiitana kuti ndikhale mtumwi, nandipatula kuti ndikalalike Uthenga wake Wabwino. Uthengawu Iye adaulonjeza kale kudzera mwa aneneri ake ndipo udalembedwa m'Malembo Oyera. Umasimba za Mwana wake, Yesu Ambuye athu. Poyang'anira umunthu wake, kholo lake ndi Davide, koma poyang'anira kuyera kwake kwaumulungu, kuuka kwake kwa akufa kukutsimikiza kuti Yesuyo ndi Mwana wa Mulungu. Mwa Khristuyo ife tidalandira mwai wokhala atumwi, kuti tithandize anthu a mitundu yonse kumkhulupirira ndi kumumvera, kuti choncho dzina lake lilemekezedwe. Ena mwa anthuwo, ndinu amene Mulungu adakuitanani kuti mukhale ake a Yesu Khristu. Ndikulembera inu nonse amene muli ku Roma, amene Mulungu amakukondani, ndipo adakuitanani kuti mukhale anthu akeake. Mulungu Atate athu ndi Ambuye athu Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere. Poyamba ndikuthokoza Mulungu wanga mwa Yesu Khristu chifukwa cha inu nonse, pakuti pa dziko lonse lapansi anthu akusimba za chikhulupiriro chanu. Mulungu ndi mboni yanga. Ndimamtumikira ndi mtima wanga wonse, pakulalika Uthenga Wabwino wonena za Mwana wake. Akudziŵa kuti ndimakukumbukirani kosalekeza m'mapemphero anga onse. Ndimampempha Mulunguyo kuti ndipeze mpata tsopano woti ndibwere kwanuko. Ndikulakalakadi kukuwonani, kuti ndikugaŵireni mphatso zina zauzimu, kuti motero ndikulimbikitseni. Makamaka ndinene kuti tikalimbikitsane pamene ndidzakhale pakati panu. Inu mudzandilimbikitsa ndi chikhulupiriro chanu, ine nkukulimbikitsani ndi chikhulupiriro changa. Abale, ndifuna kuti mudziŵe kuti kaŵirikaŵiri ndakhala ndikuganiza zobwera kwanuko, koma mpaka tsopano panali zina zondiletsa. Ndifuna kuti pakati panuponso ndidzagwire ntchito yoonetsa zipatso, monga zidachitikira pakati pa anthu enanso a mitundu ina. Ndili ndi udindo wolalikira anthu ovumbuluka ndi osavumbuluka, ndiwo anzeru ndi opulukira omwe. Chimenechi ndicho chikundikakamiza kukalalika Uthenga Wabwino kwa inunso a ku Roma. Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino ai, chifukwa Uthengawo ndi mphamvu ya Mulungu yopulumutsa munthu aliyense wokhulupirira, poyamba Ayuda, pambuyo pake anthu a mitundu ina. Uthengawutu umatiwululira m'mene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pa Mulungu. Njira yake kuyambira pa chiyambi mpaka potsiriza ndi yakuti anthu akhulupirire. Paja Malembo akuti, “Munthu wolungama pakukhulupirira adzakhala ndi moyo.” Mkwiyo wa Mulungu ukuwoneka kuchokera Kumwamba. Amakwiyira anthu chifukwa cha kusalungama kwao konse ndi kusamchitira ulemu. Kusalungama kwaoko kumaŵalepheretsa kudziŵa zoona. Mulungu amaŵakwiyira, chifukwa zimene munthu angathe kudziŵa zokhudza Mulungu iwo akuzidziŵa bwino lomwe, popeza kuti Mulungu mwini ndiye adaŵaululira zimenezi. Pajatu chilengedwere cha dziko lapansi anthu akhala akuzindikira makhalidwe osaoneka a Mulungu, ndiye kuti mphamvu zake zosatha, ndiponso umulungu wake. Akhala akuzizindikira poona zimene Mulungu adalenga. Choncho alibe konse pozembera. Inde ankamudziŵa Mulungu, koma m'malo mwa kumtamanda kapena kumthokoza, maganizo ao adasanduka opanda pake, ndipo m'mitima yao yopusa mudadzaza mdima. Iwo amadziyesa anzeru, koma chikhalirecho ndi opusa. Adaleka kulemekeza Mulungu wosafa, nkumapembedza mafano ooneka ngati munthu amene amafa, kapena ngati mbalame ndi nyama zina, kapena zokwaŵa. Nchifukwa chake Mulungu adaŵasiya kuti azingochita zonyansa zimene mitima yao inkalakalaka, mpaka kunyazitsa matupi ao. Adasiya zoona za Mulungu namatsata zabodza. Adayamba kupembedza ndi kutumikira zolengedwa m'malo mwa kupembedza ndi kutumikira Mlengi mwini, amene ali woyenera kumlemekeza mpaka muyaya. Amen. Chifukwa cha zimenezi Mulungu adaŵasiya kuti azitsata zilakolako zochititsa manyazi. Ngakhale akazi omwe adaleka machitidwe achibadwa pa zachikwati, namatsata machitidwe ena otsutsana ndi achibadwawo. Chimodzimodzinso amuna, adaleka machitidwe achibadwa osirira akazi, nkumakhumbana amuna okhaokha. Ankachitana zamanyazi, motero adadziitanira chilango choyenera molingana ndi zochita zao zopotokazo. Tsono popeza kuti iwo sadalabadireko za kumvera Mulungu, Mulunguyo adaŵasiya m'maganizo ao opusa, kotero kuti amachita zosayenera. Mitima yao idadzaza ndi zosalungama zamitundumitundu, monga kuipa, umbombo ndi dumbo. Amangolingalira za kaduka, za kupha anthu, za ndeu, za kunyenga, ndi za njiru. Amachita ugogodi, amasinjirira, ndipo amadana ndi Mulungu. Ndi achipongwe, odzikuza, ndi onyada. Amafunafuna njira zatsopano zochitira zoipa, samvera makolo ao. Ndi opusa, osakhulupirika, okhakhala moyo, ndi opanda chifundo. Amalidziŵa lamulo la Mulungu lakuti anthu ochita zotere ndi oyenera kufa, komabe iwo omwe amachita zomwezo, ndiponso amavomerezana ndi anthu ena ozichita. Tsono woweruza enawe, kaya ndiwe yani, ulibe pozembera. Pakutitu pamene ukuweruza mnzako, ukudzitsutsa wekha, popeza kuti iweyo woweruzawe umachita zokhazokhazo. Tikudziŵa kuti Mulungu salakwa akamaweruza anthu ochita zotere. Tsono mnzangawe amene umaweruza ena ochita zimenezi, pamene iwenso umachita zomwezo, kodi ukuganiza kuti chidzakuphonya chiweruzo cha Mulungu? Kodi kapena ukupeputsa chifundo chachikulu cha Mulungu, kuleza mtima kwake, ndi kupirira kwake? Kodi sukudziŵa kuti Mulungu akukuchitira chifundo chifukwa afuna kuti utembenuke mtima? Koma chifukwa ndiwe wa mtima wokanika ndi wosafuna kutembenuka, ukudzisungira chilango cha Mulungu. Chilangocho chidzakugwera pa tsiku limene adzaonetse mkwiyo wake ndiponso kuweruza kwake kolungama. Iye adzabwezera aliyense molingana ndi ntchito zake. Anthu amene amafunafuna ulemerero, ulemu ndi moyo pakuchita ntchito zabwino molimbikira, Mulungu adzaŵapatsa moyo wosatha. Koma ochita zaupandu, namatsutsa zoona nkumachita zosalungama, Mulungu adzaŵakwiyira ndi kuŵazazira. Masautso ndi zoŵaŵa zidzaŵagwera onse ochita zoipa, poyamba Ayuda, kenaka anthu a mitundu ina. Koma Mulungu adzaŵapatsa ulemerero, ulemu ndi mtendere onse ochita zabwino, poyamba Ayuda, kenaka anthu a mitundu inanso. Pajatu Mulungu alibe tsankho. Anthu onse amene adachimwa osadziŵa Malamulo, iwonso adzaonongeka ngakhale sadaŵadziŵe Malamulowo. Ndipo onse amene adachimwa atadziŵa Malamulo, adzaweruzidwa potsata Malamulowo. Pakuti amene ali olungama pamaso pa Mulungu si amene amangomva Malamulo chabe ai. Koma okhawo amene amachitadi zonenedwa m'Malamulo ndiwo amene Mulungu adzaŵaona kuti ngolungama. Anthu amene sali Ayuda alibe Malamulo, koma pamene mwa iwo okha amachita zimene Malamulowo anena, amaonetsa kuti ali nawo malamulo mumtima mwao, ngakhale alibe Malamulo a Mose. Ntchito zaozo zimatsimikiza kuti Malamulowo ndi olembedwa m'mitima mwao. Mitima yao yomwe imatsimikiza kuti ndi momwemodi, popeza kuti maganizo ao m'chikatikati mwina amaŵatsutsa, mwina amaŵavomereza. Monga unenera Uthenga Wabwino umene ndimalalika, zidzateronso pa tsiku lija limene Mulungu mwa Khristu Yesu adzaweruza zinsinsi za m'mitima mwa anthu. Koma tsono iweyo amene umati ndiwe Myuda, umadalira Malamulo, ndipo umanyadira Mulungu wako. Ukudziŵa zimene Mulungu afuna kuti uchite, ndipo chifukwa udaphunzira Malamulowo, umadziŵanso kusiyanitsa pakati pa zabwino ndi zoipa. Umakhulupirira kuti ndiwe mtsogoleri wa anthu akhungu, nyale younikira anthu amene ali mu mdima, mlangizi wa anthu opusa, ndiponso mphunzitsi wa anthu osadziŵa. Umatsimikiza kuti m'Malamulowo umapezamo nzeru zonse ndi zoona zonse. Tsono iwe wophunzitsa ena, bwanji sukudziphunzitsa wekha? Iwe wolalika kuti, “Osamaba,” bwanji iwenso umaba? Nanga iwe wonena kuti, “Osamachita chigololo,” bwanji iwenso umachita chigololo? Iwe amene umanyansidwa ndi mafano, bwanji umaba za m'nyumba zopembedzeramo mafanowo? Iwe wonyadira Malamulo a Mulungu, bwanji umachititsa Mulungu manyazi pakuphwanya Malamulowo? Ndi monga Malembo anenera kuti, “Anthu akunja amanyoza Mulungu chifukwa cha inu Ayudanu.” Kuumbala kwako nkopindulitsa ngati utsata Malamulo a Mulungu. Koma ngati suŵatsata Malamulowo, ukadayenera kungokhala wosaumbalatu basi. Koma ngati munthu wosaumbala atsata zimene Malamulowo anena, kodi iyeyu pamaso pa Mulungu sadzakhala ngati munthu woumbala, ngakhale ndi wosaumbala m'thupi? Nchifukwa chake wosaumbalayo amene amatsata Malamulo ndiye adzakutsutsa iwe amene uli woumbala, ndipo uli ndi Malamulo olembedwa, koma umaŵaphwanya. Myuda weniweni si amene amangooneka chabe ngati Myuda pamaso pa anthu. Ndipo kuumbala kwenikweni si kumene kumachitika m'thupi nkuwonekera ku anthu ai. Myuda weniwenitu ndi amene ali Myuda mumtima mwake, ndipo kuumbala kwenikweni ndi kwa mtima, kochitika ndi Mzimu Woyera, osati ndi Malamulo olembedwa ai. Woyamikira munthu wotere ndi Mulungu, osati anthu ai. Tsono Ayuda amaposa bwanji anthu a mitundu ina? Kapena pali phindu lanjinso pa kuumbala? Pali phindu lalikulu ndithu kukhala Myuda. Choyamba, Mulungu adapatsa Ayuda mau ake kuti aŵasunge. Nanga ngati ena mwa iwo anali osakhulupirika, kodi chifukwa cha kusakhulupirika kwaoko ndiye kuti ndi Mulungu yemwe sadzakhulupirika? Mpang'ono pomwe. Koma anthu adziŵe kuti zimene Mulungu amalankhula nzoonadi, ngakhale kuti anthu onse ndi onama. Ndi monga Malembo akunenera kuti, “Inu Mulungu, anthu adziŵe kuti mumanena zoona mukamalankhula, adziŵe kuti mumapambana mukamazenga mlandu.” Koma ngati kuipa mtima kwathu kuwonetsa kuti Mulungu ngwolungama, tinganene chiyani? Kodi tinganene kuti Mulungu ngwosalungama pamene atilanga? (Ndikulankhulatu monga momwe anthu ena amalankhulira). Mpang'ono pomwe. Mulungu akadakhala wosalungama, akadatha bwanji kukhala woweruza anthu onse? Koma wina nkunena kuti, “Nanga kunama kwanga kutaonetsa koposa kale kuti Mulungu ndi woona, ndi kuwonjezera pa ulemu wake, kodi pamenepo angandiweruze kuti ndine wochimwa?” Apo bwanji sitingonena kuti, “Tizichita zoipa kuti zabwino ziwoneke”? Alipo anthu ena amene amatisinjirira kuti timanena zotere. Iwoŵa adzalangidwa monga kuyenera. Nanga bwanji tsono? Kodi ife Ayuda tikuposa anthu a mitundu ina? Mpang'ono pomwe. Tafotokoza kale kuti onse ndi ochimwa, Ayuda ndi anthu a mitundu ina omwe. Paja Malembo akuti, “Palibe munthu wolungama, ai ndithu ndi mmodzi yemwe. Palibe munthu womvetsa, palibe munthu wofunadi kutumikira Mulungu. Onse asokera, onse pamodzi achimwa, palibe wochita zabwino, ai ndithu ndi mmodzi yemwe. M'kamwa mwao m'moopsa ngati manda apululu, ndi lilime lao amalankhula zonyenga, pamilomo pao pamatuluka mau aululu, ululu wake wonga wa mamba. M'kamwa mwao m'modzaza ndi matemberero, mumatuluka mau oŵaŵa. Amafulumira kupweteka ndi kupha anzao. Amasakaza ndi kusautsa kulikonse kumene amapita, ndipo njira yamtendere saidziŵa. Saopa Mulungu mpang'ono pomwe.” Tsono tikudziŵa kuti zonse zimene Malamulo a Mulungu anena, zimakhalira amene ali olamulidwa ndi Malamulowo. Cholinga chake nchakuti anthu onse asoŵe ponena, ndipo onse adzazengedwe ndi Mulungu. Pajatu palibe munthu amene Mulungu amamuwona kuti ngwolungama chifukwa cha kutsata Malamulo chabe. Malamulo amangotizindikiritsa kuchimwa kwathu. Koma tsopano yaoneka njira yopezera chilungamo pamaso pa Mulungu, ndipo njira yake si kutsata Malamulo ai. Malamulowo ndi aneneri omwe amaichitira umboni. Njira yake imene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pa Mulungu ndi yakuti anthuwo akhulupirire Yesu Khristu. Zimenezi Mulungu amachitira anthu onse okhulupirira Khristu. Paja palibe kusiyana pakati pa anthu ai, popeza kuti onse adachimwa, nalephera kufika ku ulemerero umene Mulungu adaŵakonzera. Koma mwa kukoma mtima kwake kwaulere, anthu amapezeka kuti ngolungama pamaso pa Mulungu, chifukwa cha Khristu Yesu amene adaŵaombola. Mulungu adampereka Iyeyu kuti ndi imfa yake akhale nsembe yokhululukira machimo a anthu omkhulupirira Iye. Mulungu adachita zimenezi kuti aonetse njira yake imene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pake. Zoonadi kale mwa kuleza mtima kwake sadalange kotheratu anthu ochimwa. Koma tsopano wapereka Yesu pofuna kutsimikiza chilungamo chake, kuti anthu adziŵe kuti Iye mwini ngwolungama, adziŵenso kuti aliyense wokhulupirira Yesu amapezeka kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu. Nanga tsono pamenepa munthu anganyadenso? Iyai, sanganyade konse. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti pamaso pa Mulungu chachikulu si ntchito zabwino zimene munthu amachita, koma chachikulu nkuti munthu azikhulupirira. Paja timaona kuti munthu amapezeka kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu pakukhulupirira, osati pakutsata Malamulo ai. Kapena Mulungu ndi Mulungu wa Ayuda okha kodi? Suja alinso Mulungu wa anthu a mitundu ina? Ndithu ndiyenso Mulungu wa anthu a mitundu ina. Paja Mulungu ndi mmodzimodzi yemweyo, mwakuti pakukhulupirira, anthu oumbalidwa amapezeka kuti ngolungama pamaso pake, nawonso osaumbalidwa, pakukhulupirira amapezeka kuti ngolungama pamaso pa Mulungu. Kodi ndiye kuti tikutaya Malamulo pamene tikunenetsa kuti pafunika chikhulupiriro? Mpang'ono pomwe. Makamaka tikuŵafikitsa pake penipeni. Tsono tinene chiyani za Abrahamu, kholo la ife Ayuda? Iyeyu adapezana ndi zotani? Chifukwa iye uja achipezeka kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu chifukwa cha ntchito zake, bwenzi atakhala nacho chifukwa chonyadira. Koma ai, pamaso pa Mulungu sangathe kunyada. Paja Malembo akuti bwanji? Akuti, “Abrahamu adakhulupirira Mulungu, ndipo pakukhulupirirapo, Mulungu adamuwona kuti ngwolungama.” Munthu akagwira ntchito, amalandira malipiro. Malipirowo sitinena kuti ndi mphatso ai, koma timati ndi zimene munthu ayeneradi kulandira chifukwa cha ntchito zake. Koma munthu atangokhulupirira, m'malo mwa kudalira ntchito zake, Mulungu amene amaŵaona kuti ngosapalamula anthu ochimwa, munthu ameneyo pakukhulupirira, Mulungu adzamuwona kuti ngwolungama pamaso pake. Davide adaanenanso zomwezo pamene adati ngwodala munthu amene Mulungu amuwona kuti ngwolungama popanda ntchito. Paja iye adanena kuti, “Ngodala anthu amene Mulungu adaŵakhululukira machimo ao, amene Iye adaŵafafanizira machimo ao. Ngwodala munthu amene Ambuye saŵerengeranso machimo ake.” Kodi madalitso ameneŵa amakhalira oumbalidwa okha, kapena ndi osaumbalidwa omwe? Amakhalira ndi osaumbalidwa omwe, popeza kuti paja Malembo tatchulaŵa akunena kuti, “Abrahamu adaakhulupirira Mulungu, tsono pakukhulupirirapo adapezeka kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu.” Nanga ndi liti zidachitika zimenezi? Kodi ndipo ataumbalidwa kapena asanaumbalidwe? Sizidachitike ataumbalidwa ai, koma asanaumbalidwe. Kuumbalidwako kudachitika pambuyo pake, kuti chikhale ngati chizindikiro chotsimikiza kuti asanaumbalidwe, adaapezeka kale kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu pakukhululirira. Motero Abrahamu ndi kholo la onse okhulupirira Mulungu, ndipo Mulungu amaŵaona kuti ngolungama, ngakhale ndi osaumbalidwa. Ndiponso ndi kholo la onse oumbalidwa, osati okhawo amene adangoumbalidwa m'thupi mokha, komanso amene akutsata chitsanzo cha chikhulupiriro cha kholo lathu Abrahamu asanaumbalidwe. Abrahamu ndi zidzukulu zake adalandira kwa Mulungu lonjezo lakuti dziko lapansi lidzakhala lao. Adalandira lonjezolo osati chifukwa cha kusunga Malamulo, koma chifukwa cha chilungamo chofumira m'chikhulupiriro. Ngati ndi odalira Malamulo okha amene adzalandire zimene Mulungu adalonjeza, ndiye kuti chikhulupiriro nchopanda pake, ndipo lonjezo lija lilibe phindu. Malamulo amangodzetsa chilango, koma kumene kulibe malamulo, kulibenso kuŵaphwanya. Nchifukwa chake lonjezolo maziko ake ndi chikhulupiriro, kuti likhale mphatso yaulere ya Mulungu, ndipo patsimikizike kuti lonjezolo adzalilandiradi anthu ofumira kwa Abrahamu. Osati okhawo amene amasunga Malamulo a Mose ai, komanso onse okhala ndi chikhulupiriro chonga cha Abrahamu. Iye ndiyedi kholo la ife tonse. Paja Malembo akuti, “Ndakuika kuti ukhale kholo la mitundu yambiri ya anthu.” Lonjezo limeneli Abrahamu adalilandira kwa Mulungu mwini amene iye ankamukhulupirira. Ndi Mulungu amene amabwezera moyo kwa akufa, ndipo amapereka moyo kwa zinthu zopanda moyo. Mulungu adati, “Zidzukulu zako zidzachulukadi.” Ndipo ngakhale zimenezi zinali zosayembekezeka konse, Abrahamu adalimbikirabe kukhulupirira kuti adzakhala kholo la mitundu yambiri ya anthu. Zaka zake zinali pafupi makumi khumi, ndipo adaadziŵa kuti thupi lake linali ngati lakufa kale, ndiponso kuti Sara anali wouma. Sadaŵakayikire konse mau a Mulunguyo, koma adalimbikira m'chikhulupiriro, nayamika Mulungu. Adakhulupirira ndithu kuti Mulungu angathe kuchita zimene adalonjeza. Nchifukwa chake, monga mau a Mulungu akunena, “Mulungu adamuwona kuti ngwolungama.” Mau a m'Malemboŵa onena kuti, “Mulungu adamuwona kuti ngwolungama,” sangonena za iye yekha ai. Akunenanso za ife amene tidzapezeka kuti ndife olungama pakukhulupirira Mulungu, amene adaukitsa Yesu Ambuye athu kwa akufa. Yesuyo adaperekedwa kuti aphedwe chifukwa cha zochimwa zathu, ndipo adauka kwa akufa kuti tipezeke olungama pamaso pa Mulungu. Tsono, popeza kuti pakukhulupirira tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu. Iyeyo ndiye amene adatitsekulira njira kuti pakukhulupirira tilandire mwai uwu umene Mulungu amapatsa mwaulere, umene takhazikikamo tsopano. Motero timakondwerera chiyembekezo chathu chakuti tidzalandirako ulemerero wa Mulungu. Koma si pokhapo ai, timakondweranso m'masautso athu. Pakuti tikudziŵa kuti masautso amaphunzitsa munthu kupirira, kupirira kumabweretsa makhalidwe ovomerezedwa ndi Mulungu, ndipo makhalidwe ovomerezedwawo amabweretsa chiyembekezo. Chiyembekezo chimenechi munthu sichingamugwiritse fuwa lamoto ai, pakuti Mulungu mwa Mzimu Woyera amene Iye adatipatsa, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake. Pa nthaŵi imene Mulungu adaikonzeratu, pamene ife tikusoŵabe pogwira, Khristu adatifera anthu ochimwafe. Nchapatali kuti munthu afere munthu wina, ngakhale winayo akhale wolungama. Kaya kapena mwina munthu nkulimba mtima mpaka kufera munthu wabwino. Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera. Ndiye popeza kuti tsopano chifukwa cha magazi ake tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, Iyeyo adzatipulumutsa koposa pamenepo ku mkwiyo wa Mulungu. Ife tinali adani a Mulungu, koma imfa ya Mwana wake idatiyanjanitsa ndi Iye. Tsono popeza kuti imfa ya Khristu idatiyanjanitsa ndi Mulungu, nanji tsono moyo wake, ndiye udzatipulumutsa kwenikweni. Koma si pokhapo ai, timakondwera mwa Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu, amene atiyanjanitsa ndi Mulungu tsopano. Uchimo udaloŵa m'dziko lapansi chifukwa cha munthu mmodzi, ndipo uchimowo udadzetsa imfa. Motero imfa idafalikira kwa anthu onse, popeza kuti onse adachimwa. Uchimo udaalipo pa dziko lapansi Mulungu asanapereke Malamulo. Koma pamene palibe Malamulo, machimo a munthu saŵerengedwa ai. Komabe kuyambira nthaŵi ya Adamu kufikira nthaŵi ya Mose, imfa inali ndi ulamuliro pa anthu onse. Inali ndi ulamuliro ngakhalenso pa amene kuchimwa kwao kunkasiyana ndi kuchimwa kwa Adamu, amene adaphwanya lamulo la Mulungu. Adamuyo amafanizira Iye uja amene Mulungu adaati adzabwerayu. Koma sitingafananitse mphatso yaulere ya Mulungu ndi kuchimwa kwa Adamu ai. Pajatu anthu ambiri adafa chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodziyo, koma kukoma mtima kwa Mulungu, ndiponso mphatso yake yaulere, zidaposa ndithu, chifukwa zidabweretsera anthu ambiri madalitso ochuluka. Mphatso imene Mulungu adaperekayo ndiye Munthu mmodzi uja, Yesu Khristu. Palinso kusiyana pakati pa mphatso imeneyi ya Mulungu ndi zotsatira zake za kuchimwa kwa munthu mmodzi kuja. Pakuti iye uja atachimwa kamodzi, Mulungu adagamula kuti alangidwe. Koma mphatso ya kukoma mtima kwa Mulungu ndi yakuti anthu amakhala olungama ngakhale zochimwa zao zinali zambiri. Chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodzi kuja, ulamuliro wa imfa udakhazikika ponseponse. Nanji tsono zotsatira za zimene adachita Munthu mmodzi wina uja, Yesu Khristu, nzazikulu kopambana. Pakuti onse olandira madalitso a Mulungu, pamodzi ndi chilungamo chimene chili mphatso yake, adzakhala ndi moyo ndi kusanduka mafumu, kudzera mwa iyeyo. Motero, monga tchimo limodzi lidadzetsa chilango pa anthu onse, momwemonso ntchito imodzi yolungama imadzetsa chilungamo kwa anthu onse ndi kuŵapatsa moyo. Pakuti monga anthu ambiri adasanduka ochimwa, chifukwa cha kusamvera kwa munthu mmodzi uja, momwemonso anthu amapezeka kuti ngolungama, chifukwa cha kumvera kwa Munthu winanso mmodzi. Mulungu adapereka Malamulo kuti anthu azindikire kuchuluka kwa machimo ao. Koma pamene uchimo udachuluka, kukoma mtima kwa Mulungu kudachuluka koposa. Choncho monga uchimo unkalamulira anthu ndi kudzetsa imfa pa iwo, momwemonso kunali koyenera kuti kukoma mtima kwa Mulungu kulamulire pakudzetsa chilungamo kwa anthu, ndi kuŵafikitsa ku moyo wosatha mwa Yesu Khristu Ambuye athu. Tsono tinene chiyani? Kodi tinganene kuti tizingokhalabe mu uchimo kuti kukoma mtima kwa Mulungu kuchuluke? Iyai, mpang'ono pomwe. Tidachita ngati kufa nkulekana ndi uchimo. Nanga tingakhalebe mu uchimowo bwanji? Kodi inu simukudziŵa kuti tonse amene tidasanduka amodzi ndi Khristu Yesu pakubatizidwa, ndi ubatizo womwewo tidasandukanso amodzi ndi Iye mu imfa yake? Nchifukwa chake pa ubatizo tidachita ngati kufa ndi kuikidwa m'manda pamodzi naye, kuti monga Khristu adauka kwa akufa ndi mphamvu ya Atate, momwemonso ife tikhale ndi moyo watsopano. Ngati takhala amodzi ndi Khristu mu imfa yake, momwemonso tidzakhala amodzi naye pa kuuka kwa akufa, monga momwe adaukira Iyeyo. Tidziŵa kuti mkhalidwe wathu wakale udapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kuti khumbo lathu lokonda machimo liwonongeke, ndipo tisakhalenso akapolo a uchimo. Pakuti munthu akafa, ndiye kuti wamasuka ku mphamvu ya uchimo. Tsono ngati tidafa pamodzi ndi Khristu, tikhulupirira kuti tidzakhalanso ndi moyo pamodzi ndi Iye. Tikudziŵa kuti Khristu adauka kwa akufa, ndipo sadzafanso. Imfa ilibenso mphamvu pa Iye. Kufa kumene adafako kunali kufa kolekana ndi uchimo, ndipo adafa kamodzi kokhako. Tsono moyo umene ali nawo tsopano ndi moyo woperekedwa kwa Mulungu. Momwemonso inuyo mudziwone ochita ngati kufa nkulekana ndi uchimo, koma okhala ndi moyo wotumikira Mulungu, mogwirizana ndi Khristu. Nchifukwa chake musalole uchimo kuti ulamulire matupi anu otha kufaŵa, ndipo musagonjere zilakolako zake. Musapereke chiwalo chilichonse cha thupi lanu ku uchimo, kuti chigwire ntchito zotsutsana ndi chilungamo. Inu mudzipereke kwa Mulungu, monga anthu amene anali akufa, koma tsopano ali amoyo. Ndipo mupereke ziwalo zanu zonse kwa Mulungu, kuti zigwire ntchito zachilungamo. Tsono uchimo sudzakhalanso ndi mphamvu pa inu, pakuti chimene chimalamulira moyo wanu si Malamulo ai koma kukoma mtima kwa Mulungu. Bwanji tsono? Kodi tizichimwabe popeza kuti chimene chimalamulira moyo wathu si Malamulo, koma kukoma mtima kwa Mulungu? Iyai, mpang'ono pomwe. Mukudziŵa paja kuti mukadzipereka kuti mukhale akapolo a munthu nkumamumvera, ndiye kuti ndinu akapolo a munthu womumverayo. Tsono ngati ndinu akapolo a uchimo, mudzafa. Koma ngati ndinu akapolo a Mulungu, mudzakhala olungama pamaso pake. Tiyamike Mulungu! Inu kale munali akapolo a uchimo, koma tsopano mukumvera ndi mtima wonse zoona za chiphunzitso chimene mudalandira. Mudamasulidwa ku uchimo, ndipo tsopano mwasanduka atumiki a Mulungu ochita zachilungamo. Ndikukupherani fanizo la ukapololi kuti mungalephere kumvetsa bwino zimenezi. Kale munkadzipereka kuti mukhale akapolo a zonyansa ndi zosalongosoka zonkirankira. Chonchonso tsopano mudzipereke kuti musanduke atumiki a Mulungu ochita zachilungamo, kuti mukhale oyera mtima. Pamene munali akapolo a uchimo, simunkalabadirako za zimene Mulungu amati nzolungama. Nanga pamenepo mudapindula chiyani pakuchita zinthu zimene tsopano mukuchita nazo manyazi? Pajatu zimene zija mathero ake ndi imfa. Koma tsopano mwamasulidwa ku uchimo, ndipo ndinu otumikira Mulungu. Phindu lake ndi kuyera mtima, ndipo potsiriza pake kulandira moyo wosatha. Malipiro amene uchimo umalipira ndi imfa. Koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu. Abale, ndikulankhulatu ndi inu amene mumadziŵa za malamulo. Mukudziŵa bwino kuti malamulo amamkhudza munthu pokhapokha pamene munthuyo ali moyo. Mwachitsanzo, malamulo amati mkazi wokwatiwa ngwomangidwa kwa mwamuna wake, nthaŵi yonse pamene mwamuna wakeyo ali moyo. Koma mwamunayo akamwalira, mkazi uja amamasuka ku malamulo okhudza za mwamuna wake aja. Nchifukwa chake ngati adzipereka kwa mwamuna wina, pamene mwamuna wake ali moyo, mkaziyo amati ngwachigololo. Koma mwamuna wake akamwalira, mkazi uja wamasuka ku malamulo a ukwati, kotero kuti sakhala wachigololo ngati akwatiwa ndi mwamuna wina. Chimodzimodzi inunso, abale anga. Mudachita ngati kufa ndi kulekana ndi Malamulo popeza kuti ndinu ziwalo za thupi la Khristu. Motero tsopano ndinu a wina wake, ndiye kuti a Iye amene adauka kwa akufa kuti tibalire Mulungu zipatso. Pamene tinkatsata mkhalidwe wathu wachibadwa, zilakolako zoipa zimene Malamulo adaaziwutsa zinkagwira ntchito mwa ife, ndipo zidabala imfa. Koma tsopano tamasuka ku Malamulowo. Tidachita ngati kufa nkulekana ndi Malamulo amene kale ankatimanga. Tsopano Mzimu Woyera akutithandiza kutumikira Mulungu mwa njira yatsopano, osatinso mwa njira yakale ija yakungotsata Malamulo olembedwa. Tsono tinene chiyani? Kodi tinene kuti Malamulo ndi auchimo? Mpang'ono pomwe. Koma Malamulowo ndiwo adandizindikiritsa za uchimo. Pakuti sindikadadziŵa kuipa kwa kusirira, Malamulo akadapanda kunena kuti, “Usasirire”. Chifukwa cha lamuloli, uchimo udapeza mpata woutsa mwa ine khalidwe la masiriro osiyanasiyana. Pakuti ngati palibe malamulo, uchimo sungachite kanthu. Ine kale ndinali ndi moyo opanda malamulo. Koma pamene ndidayamba kudziŵa malamulo, pomwepo uchimo udayamba kulimba, ndipo ine ndidakhala ngati ndafa. Tsono malamulo omwewo amene adaayenera kufikitsa anthu ku moyo, ine adandifikitsa ku imfa. Pakuti uchimo udapeza mpata chifukwa cha malamulo, ndipo mwa malamulowo udandinyenga ndi kundipha. Mosakayika konse, Malamulo a Mose ndi ochokera kwa Mulungu, ndipo lamulo lililonse mwa Malamulowo ndi loyera, lolungama ndi labwino. Kodi tsono ndiye kuti chinthu chabwinochi chidandiphetsa? Mpang'ono pomwe. Koma uchimo ndiwo udandipha pakugwiritsa ntchito chinthu chabwinocho kuti khalidwe lenileni la uchimowo liwonekere poyera kuti ndi uchimodi. Motero kudzera mwa malamulo, uchimo umaoneka woipa kopitirira. Tikudziŵa kuti Malamulo a Mose ndi opatsidwa ndi Mulungu. Koma ine ndine munthu wofooka chabe, wogulitsidwa ngati kapolo ku uchimo. Sindimvetsa bwino zimene ndimachita. Pakuti sindichita zimene ndifuna kuchita, koma zomwe ndimadana nazo, nzimene ine ndimazichita. Koma ngati sindifuna kuchita zoipa zimene ndimachita, ndiye kuti ndikuvomereza kuti Malamulo aja ndi abwino. Motero zimene zimachitikazo, sindine amene ndimazichita, koma uchimo umene umakhala mwa ine. Ndikudziŵa kuti mwa ine simukhala kanthu kabwino. Ndikamati, “ine”, ndikunena khalidwe langa lokonda zoipa. Ngakhale ndimafuna kuchita zabwino, komabe sindizichita. Sindichita zabwino zimene ndifuna, koma ndimachita zoipa zimene sindifuna. Ngati ndichita zimene sindizifuna, sindinenso amene ndimazichita, koma uchimo umene umakhala mwa ine. Motero ndimaona kuti chimene chimachitika nchakuti pamene ndifuna kuchita zabwino, zoipa zili nane pomwepo. Mtima wanga umakondwa ndi Malamulo a Mulungu, koma m'kati mwanga ndimaona lamulo lina lolimbana ndi lamulo limene mtima wanga wavomereza. Lamulo limenelo landisandutsa kapolo wa lamulo la uchimo lokhala m'kati mwanga. Kalanga ine! Ndani adzandipulumutsa ku khalidwe langa lino londidzetsera imfa? Tiyamike Mulungu! Adzandipulumutsa ndiye kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye athu. Motero ineyo, ndi mtima wanga ndimatumikira Malamulo a Mulungu, chonsecho ndi khalidwe langa lokonda zoipa, ndimatumikira lamulo la uchimo. Motero tsopano palibiretu mlandu wotsutsa anthu amene amakhala mwa Khristu Yesu. Pakuti lamulo la Mzimu Woyera, lotipatsa moyo mwa Khristu Yesu, landimasula ku lamulo la uchimo ndi la imfa. Mulungu adachita zimene Malamulo a Mose sadathe kuzichita, chifukwa khalidwe la anthu lopendekera ku zoipa lidaŵafooketsa. Iye adatsutsa uchimo m'khalidwe lopendekera ku zoipalo, pakutuma Mwana wakewake, ali ndi thupi longa la ife anthu ochimwa, kuti m'thupilo adzagonjetse uchimowo. Mulungu adachita zimenezi, kuti chilungamo chimene Malamulo a Mose amatipempha, chiwoneke kwathunthu mwa ife amene sitimveranso khalidwe lathu lopendekera ku zoipa, koma timamvera Mzimu Woyera. Anthu omvera khalidwe loipalo, amaika mtima pa zilakolako zathupi. Koma anthu omvera Mzimu Woyera, amaika mtima pa zimene Mzimu Woyerayo afuna. Kuika mtima pa khalidwe lopendekera ku zoipa, ndi imfa yomwe, koma kuika mtima pa zimene Mzimu Woyera afuna, kumabweretsa moyo ndi mtendere. Anthu oika mtima pa khalidwe lokonda zoipa, amadana ndi Mulungu. Anthu otere sagonjera Malamulo a Mulungu, ndipo kunena zoona, sangathedi kuŵagonjera. Ndipo anthu oika mtima pa khalidwe limenelo, sangathe kukondweretsa Mulungu. Koma inu simulamulidwanso ndi khalidwe lanu lopendekera ku zoipa. Mumalamulidwa ndi Mzimu Woyera, ngati Mzimu wa Mulungu akhaladi mwa inu. Koma ngati munthu aliyense alibe Mzimu wa Khristu, iyeyu sali wake wa Khristu. Khristu akakhala mwa inu, ngakhale thupi lanu lidzafadi chifukwa cha uchimo, komabe mzimu wanu udzakhala ndi moyo, popeza kuti Mulungu wakuwonani kuti ndinu olungama pamaso pake. Ndipo Mzimu wa Mulungu, amene adaukitsa Yesu kwa akufa, akamakhala mwa inu, pamenepo, mwa Mzimu wake yemweyo, Mulungu adzapatsanso moyo matupi anu otha kufaŵa. Motero abale, tili ndi ngongole, komatu ngongole yake si yakuti tizigonjera khalidwe lathu lokonda zoipa, ndi kumachita chifuniro chake. Pakuti ngati m'moyo mwanu mutsata khalidwelo, mudzafa. Koma ngati ndi chithandizo cha Mzimu Woyera mupha zilakolako zanu zathupi, mudzakhala ndi moyo. Onse amene Mzimu wa Mulungu amaŵatsogolera, amenewo ndi ana a Mulungu. Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, “Abba! Atate!” Mzimu Woyera mwiniwakeyo ndi amene amavomerezana ndi mitima yathu kutsimikiza kuti ndife ana a Mulungu. Tsono ngati ndife ana a Mulungu, tidzalandira nao madalitso amene Iye akusungira anthu ake. Pamodzi ndi Khristu ifenso tidzalandira madalitso amene Mulungu anali atamsungira. Pakuti ngati timva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye. Ine ndikutsimikiza kuti masautso amene tikuŵamva tsopano salingana mpang'ono pomwe ndi ulemerero umene Mulungu adakonza kuti adzatiwonetse m'tsogolo muno. Zolengedwa zonse zikudikira molakalaka kuti Mulungu aonetse ana ake poyera. Pakuti zolengedwazo zidaasanduka zogonjera zopanda pake, osati chifukwa zidaafuna kutero ai, koma chifukwa Mulungu adaagamula choncho. Komabe zili ndi chiyembekezo ichi, chakuti izonso zidzamasulidwa ku ukapolo wa kuwola, ndi kulandirako ufulu ndi ulemerero wa ana a Mulungu. Tikudziŵa kuti mpaka tsopano zolengedwa zonse zakhala zikubuula ndi kumva zoŵaŵa, zonga za mkazi pa nthaŵi yake yochira. Tsonotu si zolengedwa zokhazi zikubuula ai. Koma ngakhale ifenso amene tili ndi mphatso zoyamba za Mzimu Woyera, tikubuula mu mtima, podikira kuti Mulungu atilandire ngati ana ake, ndi kupulumutsa matupi athu omwe. Inde, Mulungu adatipulumutsa, koma tikuyembekezabe chipulumutsocho. Koma tsono tikamaona ndi maso zimene tikuziyembekezazi, apo si chiyembekezonso ai. Koma ngati tiyembekeza zimene sitidaziwone ndi maso, timazidikira mopirira. Momwemonso Mzimu Woyera amatithandiza. Ndife ofooka, osadziŵa m'mene tiyenera kupempherera. Nchifukwa chake Mzimu Woyera mwiniwake amatipempherera ndi madandaulo osafotokozeka. Ndipo Mulungu amene amayang'ana za m'kati mwa mitima ya anthu, amadziŵa zimene Mzimu Woyera afuna, pakuti Mzimuyo amapempherera anthu a Mulungu monga momwe Mulungu afunira. Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera. Pakuti anthu amene Mulungu adaŵasankhiratu, Iye adaŵapatulanso kale kuti akhale monga Mwana wake, kuti choncho Mwanayo akhale woyamba mwa abale ambiri. Mulungu sadangoŵapatula, komanso adaŵaitana. Sadangoŵaitana, komanso adaŵaona kuti ngolunga pamaso pake. Ndipo sadangoona kuti ngolunga pamaso pake, komanso adaŵagaŵirako ulemerero wake. Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani? Iye sadaumire ngakhale Mwana wakewake, koma adampereka chifukwa cha ife tonse. Atatipatsa Mwana wakeyo, nanga Iye nkulephera kutipatsanso zonse mwaulere? Ndani angaŵaimbe mlandu anthu amene Mulungu adaŵasankha? Mulungu mwiniwake amaŵaona kuti ngolungama pamaso pake. Tsono palibe amene angaŵaweruze kuti ngopalamula. Khristu Yesu amene adafa, kaya tinene kuti amene adauka kwa akufa, amenenso ali ku dzanja lamanja la Mulungu, ndiye amene akutinenera kwa Mulunguyo. Tsono ndani angatilekanitse ndi chikondi cha Khristu? Kodi ndi masautso, kapena zoŵaŵa, kapena mazunzo, kapena njala, kapena usiŵa, kapena zoopsa, kapenanso kuphedwa? Paja Malembo akuti, “Chifukwa cha Inu tsiku lonse akufuna kutipha, pamaso pao tili ngati nkhosa zimene akukazipha.” Koma pa zonsezi tili opambana ndithu chifukwa cha Iye amene adatikonda. Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu. Ndithudi ndikunena zoona ine amene ndili wake wa Khristu, ndipo sindikunama ai. Mtima wanga, umene Mzimu Woyera amautsogolera, ukundichitira umboni kuti ndili ndi chisoni chachikulu. Ndipo ukundipweteka kosalekeza chifukwa cha abale anga, anthu a mtundu wangaŵa. Ndikadakonda kuti m'malo mwao, ineineyo ndikhale wotembereredwa, osakhalanso wake wa Khristu. Iwoŵa ndi Aisraele, amene Mulungu adaŵasankha kuti akhale ana ake, ndipo adaŵapatsa ulemerero. Mulungu adachita nawo mapangano, ndipo adaŵapatsa Malamulo ake. Adaŵaphunzitsa mwambo wachipembedzo, ndipo adaŵapatsa malonjezo ake. Iwoŵa ndi zidzukulu za makolo athu akale aja, ndipo Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndi wa mtundu wao, kunena za umunthu wake. Mulungu amene amalamulira zonse, alemekezeke mpaka muyaya. Amen. Sindiye kutitu Mulungu sadasunge malonjezo ai. Pakuti si anthu onse obadwa mu mtundu wa Aisraele amene ali Aisraele enieni. Ndiye kuti si zidzukulu zonse za Abrahamu zimene zili ana a Mulungu. Koma Mulungu adauza Abrahamu kuti, “Ana a Isaki okha ndiwo adzatchedwa zidzukulu zako.” Ndiye kuti, si ana onse a Abrahamu amene ali ana a Mulungu ai. Zidzukulu zake zenizeni ndi ana okhawo amene adabadwa potsata lonjezo la Mulungu. Paja Mulungu adalonjeza pakunena kuti, “Ndidzabwera pa nthaŵi yake ndipo Sara adzakhala ndi mwana.” Ndipo si pokhapo ai. Ana aŵiri a Rebeka aja bambo wao anali mmodzi, kholo lathu Isaki. Ngakhale anawo asanabadwe, ndiye kuti tsono asanachite chilichonse chabwino kapena choipa, Mulungu adaafunabe kuti cholinga chake chosankhira munthu aliyense chipitirire. Izi adachita osati chifukwa cha ntchito za munthu koma chifukwa chakuti Mulungu adamuitana munthuyo. Motero Mulungu adauza Rebeka kuti, “Wamkuluyu adzatumikira wamng'onoyu.” Paja Malembo akuti, “Yakobe ndidaamukonda, koma Esau ndidaadana naye.” Pamenepo tinganene chiyani tsono? Kodi tinganene kuti Mulungu ngwosalungama? Iyai, sitingatero. Pajatu Iye adaauza Mose kuti, “Ndidzachitira chifundo amene ndifuna kumchitira chifundo, ndidzamvera chisoni amene ndifuna kumumvera chisoni.” Motero chachikulu si zimene munthu azifuna, kapena zimene munthu amayesetsa kuchita, koma chachikulu ndi chifundo cha Mulungu. Ndi monga m'Malembo timaŵerenga kuti Mulungu adaauza Farao kuti, “Ndidakulonga ufumu, kuti mwa iwe ndiwonetse mphamvu zanga, ndiponso kuti ndimveketse dzina langa pa dziko lonse lapansi.” Motero timaona kuti Mulungu amachitira chifundo munthu amene Iye afuna kumchitira chifundo, ndipo amamsandutsa wokanika munthu amene Iye afuna kumsandutsa wokanika. Tsono kapena wina nkundifunsa kuti, “Ngati zili choncho, chifukwa chiyani Mulungu akuŵadzudzulabe anthu? Nanga ndani angaletse Mulungu kuchita zimene Iye afuna?” Koma iwe, munthu chabe, ndiwe yani kuti nkumatsutsana ndi Mulungu? Kodi mbiya nkufunsa woiwumba kuti, “Bwanji mwandiwumba motere?” Kodi kapena woumba sangathe kuumba mbiya ziŵiri ndi dothi lomwelo, ina ya masiku apadera ina ya masiku onse? Mulungunso ndi momwemo. Adaafuna kuwonetsa mkwiyo wake, nafunanso kuti mphamvu zake zidziŵike. Komabe adapirira moleza mtima kwambiri zochita za anthu amene Iye adaaŵakwiyira, ndipo amene adaayeneradi kuwonongedwa. Mulungu adaafunanso kuti udziŵike ulemerero wake waukulu pa ife, amene Iye adatichitira chifundo, natikonzeratu kuti tilandire ulemerero. Pajatu ife ndife amene Mulungu adatiitana, osati kuchokera kwa Ayuda okha ai, komanso kuchokera kwa anthu a mitundu ina. Ndi monga momwe Mulungu akunenera m'buku la mneneri Hoseya kuti, “Amene sanali anthu anga, ndidzaŵatcha ‘Anthu anga’. Mtundu umene sindinkaukonda, ndidzautcha ‘Wokondedwa wanga’. Ndipo kumalo komwe iwo adauzidwa kuti, ‘Sindinu mtundu wanga’, kumeneko adzatchedwa ‘Ana a Mulungu wopatsa moyo.’ ” Ndipo mneneri Yesaya adaanena mokweza mau za Aisraele kuti, “Ngakhale Aisraele achuluke ngati mchenga wakunyanja, koma oŵerengeka okha adzapulumuka. Pakuti Ambuye adzagamula milandu ya anthu pa dziko lapansi. Ndipo adzachita zimenezi mofulumira ndi mwachidule.” Izi zili monga momwe Yesaya adaaneneratunso kale kuti, “Ambuye amphamvuzonse akadapanda kutisiyirako zidzukulu zina, tikadafafanizidwa ngati Sodomu ndi Gomora.” Tsono pamenepo tinene chiyani? Tinene kuti anthu a mitundu ina, amene sankalabadira zoti akhale olungama pamaso pa Mulungu, adachilandira chilungamocho pakukhulupirira. Koma Aisraele amene ankayesetsa kukhala olungama pamaso pa Mulungu pakusunga Malamulo a Mose, adalephera. Chifukwa chiyani? Chifukwa ankafuna kupezeka kuti ngolungama pamaso pa Mulungu, osati pakukhulupirira, koma pakudalira ntchito zabwino. Adaphunthwa pa mwala wophunthwitsa anthu, monga Malembo anenera kuti, “Inetu ndikuika m'Ziyoni mwala wodzakhumudwitsa anthu, thanthwe limene lidzaŵagwetsa. Koma wokhulupirira Iyeyo, sadzachita manyazi.” Abale, chimene ndimakhumbitsa ndi mtima wanga wonse, ndipo chimene ndimapempha Mulungu, ndi chakuti Aisraele apulumuke. Ndikuŵachitira umboni kuti ndi achangudi pa zinthu za Mulungu, koma changu chake sadachimvetse bwino m'mene chiyenera kukhalira. Sadziŵa chilungamo chochokera kwa Mulungu, koma adayesa kupezeka kuti ngolungama pamaso pake mwa njira yaoyao, osagonjera chilungamo chochokera kwa Mulungu. Khristu adafikitsa Malamulo a Mose ku mapherezero, kotero kuti aliyense wokhulupirira, amapezeka kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu. Kunena za chilungamo chimene chimapezeka pakumvera Malamulo, Mose adalemba kuti, “Munthu wochita zimene Malamulo amanena, adzakhala ndi moyo pakuzichita.” Koma kunena za chilungamo chimene chimapezeka pakukhulupirira, akuti, “Mumtima mwako usanene kuti, ‘Ndani adzakwera Kumwamba?’ ” (Ndiye kuti kukamuuza Khristu kuti atitsikire ife.) “Usanenenso kuti, ‘Ndani adzatsikira ku dziko la anthu akufa?’ ” (Ndiye kuti kukamubwezera Khristu kuchokera ku dziko la anthu akufa.) Koma nanga akuti chiyani? Akuti, “Mau sali nawe kutali, ali pakamwa pako, ndiponso mumtima mwako.” (Ameneŵa ndiwo mau a chikhulupiriro amene timaŵalalika.) Ngati uvomereza ndi pakamwa pako kuti Yesu ndi Ambuye, ndipo ukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu adamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka. Chifukwa munthu amati akakhulupirira ndi mtima wake, amapezeka wolungama pamaso pa Mulungu, ndipo amati akavomereza chikhulupiriro chakecho ndi pakamwa pake, amapulumuka. Paja Malembo akuti, “Munthu aliyense wokhulupirira Iye, sadzachita manyazi.” Choncho palibe kusiyana pakati pa Ayuda ndi anthu a mitundu ina, pakuti Mulungu ndiye Ambuye a onse, ndipo amadalitsa mooloŵa manja onse otama dzina lake mopemba. Ndi monga momwe mau a Mulungu anenera kuti, “Aliyense amene adzatama dzina la Ambuye mopemba adzapulumuka.” Kodi anthu angatame Mulungu bwanji mopemba ngati sadamkhulupirire? Ndipo angamkhulupirire bwanji ngati sadamve za Iye? Ndipo angamve za Iye bwanji ngati palibe wina wolalika? Ndipo anthu angalalike bwanji ngati palibe oŵatuma? Paja mau a Mulungu akuti, “Nchokondweretsa zedi kuwona olalika Uthenga Wabwino akufika.” Koma si onse amene adalandira Uthenga Wabwinowo. Ndi monga mneneri Yesaya anenera kuti, “Ambuye, ndani adakhulupirira zimene tidalalika?” Motero munthu amakhulupirira chifukwa cha zimene wamva, ndipo zimene wamvazo zimachokera ku zolalika za Khristu. Koma ntafunsa: kodi ndiye kuti Aisraele sadaŵamve mauwo? Iyai, kumva adamva ndithu. Ndi monga mau a Mulungu anenera kuti, “Liwu lao lidamveka pa dziko lonse lapansi, mau ao adafika mpaka ku malekezero a dziko.” Ntafunsanso: monga nkuti Aisraele sadaŵamvetse mauwo? Mose ndiye woyamba kuyankhapo. Iye adati, “Ndidzakuchititsani kaduka ndi mtundu umene suli mtundu weniweni, ndidzakukwiyitsani ndi mtundu wa anthu opusa.” Ndipo Yesaya adaanena molimba mtima kuti, “Adandipeza anthu amene sanali kundifunafuna. Ndidaŵaonekera anthu amene sankafunsa za Ine.” Koma za Aisraele adati, “Tsiku lonse ndidatambalitsa manja anga kwa mtundu wa anthu osandimvera ndi ondiwukira Ine.” Tsono ndikufunsa kuti, “Kodi Mulungu adataya anthu ake?” Iyai, chosatheka! Inenso ndine Mwisraele, mmodzi mwa zidzukulu za Abrahamu, ndiponso wa fuko la Benjamini. Mulungu sadaŵataye anthu ake amene Iye adaŵasankha kale. Monga simudziŵa mau aja a m'Malembo, pamene mneneri Eliya akudandaula kwa Mulungu kuti aŵalange Aisraele? Paja adati, “Ambuye, anthu ameneŵa adapha aneneri anu, nagwetsa maguwa anu ansembe. Ndatsala ine ndekha, ndipo akufuna kupha ndi ine ndemwe.” Koma Mulungu adamuyankha chiyani? Adati, “Ndadzisungira anthu zikwi zisanu ndi ziŵiri amene sadapembedzepo Baala, mulungu wonama uja.” Tsono ndi momwemonso makono. Patsala Aisraele oŵerengeka amene Mulungu adaŵasankha mwa kukoma mtima kwake. Komatu ngati adaŵasankha chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye kuti si chifukwa cha zimene iwo adaachita. Zikadatero, kukoma mtima kwake sikukadakhalanso kukoma mtima ai. Bwanji tsono? Aisraele sadapeze zimene ankafunafuna. Koma anthu pang'ono chabe amene Mulungu adaŵasankha ndiwo adazipeza. Otsalawo adagontha m'khutu, monga Malembo anenera kuti, “Mulungu adaŵapatsa mtima wosatha kumvetsa zinthu, ndipo mpaka lero lino waŵasandutsa osatha kupenya ndi osatha kumva.” Ndipo Davide akuti, “Maphwando ao asanduke msampha ndi diŵa loŵakola, ndi kuŵagwetsa kuti alangidwe. Maso ao atsekedwe kuti asapenye, ndipo msana wao ukhale wopindika nthaŵi zonse.” Tsono ndikufunsa kuti, “Kodi Ayuda adaphunthwa kuti agweretu osadzukanso?” Mpang'ono pomwe. Koma chifukwa cha kuchimwa kwa Ayudawo, chipulumutso chidafikiranso anthu a mitundu ina, kuti Ayuda aŵachitire nsanje. Ngati kuchimwa kwa Ayuda kudapindulitsa anthu a pa dziko lonse lapansi, ndipo ngati kulephera kwao kudapindulitsa kwakukulu anthu a mitundu ina, nanji tsono onse akadzamvera Mulungu, ndiye kuti madalitso adzakula zedi. Tsopano ndifuna kukuuzani kanthu, inu amene simuli Ayuda. Malinga nkuti ndine wotumidwa kwa anthu a mitundu ina, ndimaunyadira utumiki wanga umenewu. Koma ndimakhumba kuti ndichititse nsanje anthu a mtundu wanga, ndi kupulumutsa ena mwa iwo. Ngati anthu a pa dziko lonse lapansi adayanjanitsidwa ndi Mulungu chifukwa Iye adaŵaika pambali Ayuda, nanga kudzatani Iye akadzaŵalandiranso? Kudzakhala monga ngati anthu akufa akuuka! Ngati munthu apatulira Mulungu chigawo chimodzi cha buledi, ndiye kuti yenseyo ndi wopatulika. Ndipo ngati muzu wa mtengo ndi wopatulika, ndiye kuti ndi nthambi zake zomwe nzopatulika. Nthambi zina za mtengo wobzala wa olivi zidakadzuka, ndipo pamalo pa nthambi zimenezo adalumikizapo kanthambi ka mtengo wa olivi wakuthengo. Ndiye kuti inu amene simuli Ayuda, muli ngati kanthambi ka mtengo wa olivi wakuthengo uja, ndipo tsopano mukulandira nao mphamvu ya m'mizu ya mtengo wobzala wa olivi, ndiye kuti Ayuda. Nchifukwa chake musamaŵanyoze amene adakadzuka monga nthambi zija. Kodi inu mungadzitame bwanji? Inutu ndinu kanthambi chabe. Sindinu amene mumagwirizira muzu ai, koma muzu ndiwo umene umagwirizira inu. Tsono mudzati, “Koma nthambi zija zidakadzuka kuti andilumikizepo ineyo pamtengopo.” Nzoona, iwo adakadzukadi chifukwa sadakhulupirire, ndipo inu pakukhulupirira, mukukhala mu mtengo tsopano. Komatu tsono musamadzitame, makamaka muzichita mantha. Mulungu sadaŵalekerere Ayuda, amene ali ngati nthambi zenizeni za mtengo. Kodi tsono mukuyesa kuti adzakulekererani inuyo? Pamenepo zindikirani kuti Mulungu ndi wachifundodi, komanso ndi waukali. Kwa anthu amene adagwa, ndi wokwiya, koma kwa inu ndi wachifundo, malinga mukasamala chifundo chake. Ngati simuchita zimenezi, adzakudulani inunso. Ndipo ngati enawo aleka kusakhulupirira kwao, adzaŵalumikizanso ku mtengo. Pakuti Mulungu ndi wamphamvu, atha kuŵalumikizanso. Inu, amene muli nthambi ya mtengo wa olivi wakuthengo, Mulungu adakukadzulani ku mtengo umene udaakubalani, nakulumikizani ku mtengo wa olivi wobzala. Ngati zili choncho, kodi sikudzakhala kwapafupi kwa Iye kuti alumikizenso ku mtengo wa olivi wobzala, nthambi zakezake zimene zidakadzuka? Pali chinsinsi, chimene ndifuna kuti muchidziŵe, kuwopa kuti mungamadziyese anzeru. Chinsinsicho ndi chakuti Aisraele ena adzapulupudza, mpaka nthaŵi imene chiŵerengero cha akunja otembenukira kwa Mulungu chidzakwanire. Pamenepo Aisraele onse adzapulumuka. Ndi monga Malembo anenera kuti, “Mpulumutsi adzachokera ku Ziyoni, adzachotsera zidzukulu za Yakobe kuipa kwao konse. Ndidzapangana nawo chipangano chimenechi ndikadzaŵachotsera machimo ao.” Chifukwa chokana Uthenga Wabwino, Ayuda asanduka adani a Mulungu, kuti inu mupindulepo. Koma ngati Mulungu adaŵasankha, iwo ndi abwenzi ake chifukwa cha makolo ao akale aja. Pakuti Mulungu sasinthanso ataitana munthu ndi kumpatsa mphatso. Kale inu a mitundu ina simunkamvera Mulungu, koma tsopano Mulungu akukuchitirani chifundo chifukwa cha kusamvera kwa Ayuda. Momwemonso Ayuda tsopano samvera Mulungu, koma cholinga chake nchakuti iwonso adzalandire chifundo pa nthaŵi yake, chifukwa cha chifundo mwalandira inuchi. Mulungu adasandutsa anthu onse akaidi a kusamvera, kuti Iye athe kuchitira onse chifundo. Chuma cha Mulungu nchachikulu zedi. Nzeru zake ndi kudziŵa kwake nzozama kwambiri. Ndani angamvetse maweruzidwe ake, ndipo njira zake ndani angazitulukire? Ndi monga mau a Mulungu anenera kuti, “Ndani amadziŵa maganizo a Chauta, ndani angamupatse malangizo? Ndani adaayamba waperekapo kanthu kwa Mulungu, kuti Mulunguyo amubwezereko kanthu?” Paja zinthu zonse nzochokera kwa Iye, nzolengedwa ndi Iye ndipo zimalinga kwa Iye. Ulemerero ukhale wake mpaka muyaya. Amen. Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu. Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa. Popeza kuti mwa kukoma mtima kwake Mulungu adandiitana kuti ndikhale mtumwi, ndikukuuzani inu nonse kuti musadziyese anzeru koposa m'mene muliri. Makamaka maganizo anu akhale odzichepetsa, molingana ndi kukula kwa chikhulupiriro chimene Mulungu wapatsa aliyense mwa inu. M'thupi lathu limodzi lomweli tili ndi ziwalo zambiri, ndipo ziwalozo zili ndi ntchito zosiyanasiyana. Momwemonso ife, ngakhale tili ambiri, ndife thupi limodzi, olumikizana mwa Khristu, ndipo tonse, aliyense pa mbali yake, ndife ziwalo zolumikizana. Tili ndi mphatso zosiyanasiyana malinga ndi m'mene Mulungu adatigaŵira mwa kukoma mtima kwake. Ngati mphatso yathu nkulalika mau a Mulungu, tiigwiritse ntchito molingana ndi chikhulupiriro chathu. Ngati mphatso yathu nkutumikira, titumikire ndithu. Ngati nkuphunzitsa, tiphunzitse ndithu. Ngati nkulimbikitsa ena, tiŵalimbikitse ndithu. Wogaŵana ndi anzake zimene ali nazo, azichita moolowa manja. Amene ali mtsogoleri, azigwira ntchito yake mwachangu. Wochitira ena chifundo, azichita mokondwa. Chikondi chizikhala chopanda chiphamaso. Muzidana ndi zoipa, nkumaika mtima pa kuchita zabwino. Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu. Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka. Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse. Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa. Pemphani Mulungu kuti aŵadalitse amene amakuzunzani. Ndithu, pemphani kuti aŵadalitse, osaŵatemberera ai. Muzikondwa nawo amene akukondwa, muzilira nawo amene akulira. Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru. Munthu akakuchitani choipa, musamubwezere choipa. Yesani kuchita zimene anthu onse amaziwona kuti nzabwino. Ngati nkotheka, khalani ndi mtendere ndi anthu onse, monga momwe mungathere. Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.” Koma makamaka, monga mau a Mulungu akunenera, “Ngati mdani wako wamva njala, iwe umpatse chakudya. Ngati wamva ludzu, iwe umpatse madzi akumwa. Ukatero udzamchititsa manyazi kwambiri.” Musagonjere zoipazo, koma gonjetsani zoipa pakuchita zabwino. Munthu aliyense azimvera akulu olamulira, chifukwa palibe ulamuliro umene sudachokere kwa Mulungu. Ndipo olamulira amene alipo, adaŵaika ndi Mulungu. Motero munthu wokana kumvera olamulira, akukana dongosolo limene adaliika Mulungu. Ndipo ochita zimenezi, adzadzitengera okha chilango. Olamulira sachititsa mantha anthu a makhalidwe abwino, koma a makhalidwe oipa. Kodi ufuna kukhala wosaopa wolamulira? Uzichita zolungama, ndipo iye adzakuyamikira, pakuti iyeyo ndi mtumiki wa Mulungu wokutsogolera kuchita zabwino. Koma ngati ukuchita zoipa uwope, pakuti ali ndi mphamvu ndithu zokulanga. Iye ndi mtumiki wa Mulungu wogwetsa mkwiyo wa Mulungu pa wochita zoipa, pomulanga. Nchifukwa chake muziŵamvera olamulira, osati chifukwa cha kuwopa mkwiyo wa Mulungu chabe, komanso chifukwa chomvera umboni wa mtima. Ndichonso mumakhomera msonkho: olamulira amatumikira Mulungu pamene akugwira ntchito yaoyi. Tsono muzipereka kwa onse zimene zikukhalira iwowo: msonkho kwa okhometsa msonkho, zolipira kwa oyenera kuŵalipira. Muzilemekeza oyenera kuŵalemekeza, ndi kuchitira ulemu oyenera kuŵachitira ulemu. Musakhale ndi ngongole ina iliyonse kwa munthu wina aliyense, koma kukondana kokha. Wokonda mnzake, watsata zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena. Pajatu malamulo amene amati, “Usachite chigololo, usaphe, usabe, usasirire”, ndiponso malamulo ena onse, amaundidwa mkota m'lamulo ili lakuti, “Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.” Ngati munthu akonda mnzake, sangamchite choipa ai. Nchifukwa chake amene amakonda mnzake, wasunga zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena. Muchite zimenezi chifukwa mukudziŵa kuti yafika kale nthaŵi yakuti mudzuke kutulo. Pakuti chipulumutso chili pafupi tsopano kuposa pamene tidayamba kukhulupirira. Usiku uli pafupi kutha, ndipo mbandakucha wayandikira. Tiyeni tsono tileke ntchito za mdima, tivale zida zomenyera nkhondo kutayera. Mayendedwe athu akhale oyenera, ngati a anthu oyenda usana. Pasakhale dyera kapena kuledzera, dama kapena zonyansa, ndeu kapena nsanje. Ambuye Yesu Khristu mwini akhale chida chanu chankhondo. Lekani mtima wofunafuna zosangalatsa thupi, musagonjere zilakolako zake zoipa. Mlandireni bwino munthu amene chikhulupiriro chake nchofooka, koma osati kuti mutsutsane naye pa maganizo ake. Wina amakhulupirira kuti palibe choletsa kudya chakudya chilichonse. Koma wina, amene chikhulupiriro chake nchofooka, amadya zamasamba zokha. Amene amadya chilichonse, asanyoze mnzake amene amazisala. Amene amasala zinthu zina asaweruze mnzake amene amazidya, pakuti Mulungu wamulandira. Kodi iweyo ndiwe yani kuti uweruze wantchito wamwini kuti walakwa? Mbuye wake yekha ndiye aweruze ngati iye wakhoza kapena walephera pa ntchito yake. Ndipo adzakhoza, popeza kuti Ambuye angathe kumkhozetsa. Ena amaganiza kuti tsiku lakutilakuti ndi loposa masiku ena, koma pamene ena akuganiza kuti masiku onse nchimodzimodzi. Aliyense achite monga momwe watsimikizira kwenikweni mumtima mwake. Amene amasunga tsiku lakutilakuti, amatero kuti alemekeze Ambuye. Amene amadya chilichonse, amatero kuti alemekeze Ambuye, pakuti amayamika Mulungu chifukwa cha chakudyacho. Amene amasala zina, amatero kuti alemekeze Ambuye, ndipo amayamika Mulungu pakutero. Palibe ndi mmodzi yemwe mwa ife amene amakhala moyo chifukwa cha iye yekha, kapena kufa chifukwa cha iye yekha. Tikakhala ndi moyo, moyowo ndi wa Ambuye, tikafa, timafera Ambuye. Nchifukwa chake, ngakhale tikhale ndi moyo kapena tife, ndife ao a Ambuye. Paja Khristu adamwalira nakhalanso ndi moyo, kuti akhale Mbuye wa anthu akufa ndiponso wa anthu amoyo. Tsono iwe, ukuweruziranji mbale wako? Kapena iwe winawe, ukunyozeranji mbale wako? Tonsefe tidzaima pamaso pa Mulungu kuti atiweruze. Paja Malembo akunena kuti, “Ambuye akuti, ‘Pali Ine ndemwe, anthu onse adzandigwadira ndi kuvomereza kuti ndine Mulungu.’ ” Motero aliyense mwa ife adzadzifotokozera yekha kwa Mulungu zimene adazichita. Tsono tiyeni tileke kumaweruzana. Makamaka mutsimikize kuti musachite kanthu kalikonse kophunthwitsa mbale wanu, kapena komchimwitsa. Pogwirizana ndi maganizo a Ambuye Yesu, ndikutsimikiza mosakayika konse kuti palibe chinthu chingadetse munthu pamaso pa Mulungu chifukwa wachikhudza. Koma ngati wina aganiza kuti chinthu nchomudetsa, kwa iyeyo chinthucho nchomudetsadi. Ngati ukhumudwitsa mbale wako pakudya chakudya cha mtundu wakutiwakuti, ndiye kuti sukuyendanso m'chikondi. Usamuwononge ndi chakudya chako munthu amene Khristu adamufera. Tsono musalole kuti anthu ena aziyese zoipa zinthu zimene inu mumaziwona kuti nzabwino. Mu ufumu wa Mulungu chachikulu si chakudya kapena zakumwa ai, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe, zimene Mzimu Woyera amapereka. Aliyense wotumikira Khristu motere, amakondweretsa Mulungu, ndipo amakhala wovomerezeka kwa anthu. Nchifukwa chake tsono tizifunafuna zimene zingathandize kuti pakhale mtendere ndiponso kugwirizana pakati pathu. Chakudya chisakuwonongetseni ntchito ya Mulungu. Zakudya zonse nzololedwa kuzidya, koma nkulakwa kudya chinthu chimene chingachimwitse anzathu. Nkwabwino kusadya nyama, kusamwa vinyo, ndiponso kusachita kanthu kalikonse kamene kangachimwitse mbale wako. Zimene iwe umakhulupirira pa zimenezi, zikhale pakati pa iweyo ndi Mulungu. Ngwodala amene mtima wake sumutsutsa pamene atsimikiza kuchita zakutizakuti. Koma munthu akamadya ali wokayika, waweruzidwa kale kuti ngwolakwa, popeza kuti zimene akuchita nzosagwirizana ndi zimene iye amakhulupirira kuti nzoyenera. Paja chilichonse chimene munthu achita, chotsutsana ndi zimene iye amakhulupirira, chimenecho ndi tchimo. Ife amene tili ndi chikhulupiriro champhamvu, tiziŵalezera mtima anthu ofooka, osamangodzikondweretsa tokha. Aliyense mwa ife azikondweretsa mnzake, ndi kumchitira zabwino, kuti alimbikitse chikhulupiriro chake. Pakuti Khristunso sankachita zinthu kungofuna kudzikondweretsa, koma ndi monga Malembo anenera kuti, “Chipongwe cha anthu okunyozani Inu chidafika pa Ine.” Zonse zolembedwa m'Malembo kale, zidalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembowo amatilimbikitsa ndi kutithuzitsa mtima, kuti tizikhala ndi chiyembekezo. Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu zoti athe kupirira naŵalimbitsa mtima, akuthandizeni kumvana bwino, motsata chitsanzo cha Khristu Yesu, akuthandizeni kuti ndi mtima umodzi, nonse pamodzi mulemekeze Mulungu ndi Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Tsono muzilandirana monga momwe Khristu adakulandirirani inu, kuti Mulungu alemekezedwe. Chifukwa kunena zoona, Khristu adasanduka mtumiki wa Ayuda, kutsimikiza kuti Mulungu ndi wokhulupirika. Adatsimikiza kukhulupirikako pakuchita zimene Mulungu adaŵalonjeza makolo ao akale aja, ndiponso pakupatsa anthu amene sali Ayuda chifukwa cholemekezera Mulungu kaamba ka chifundo chake. Ndi monga Malembo anenera kuti, “Nchifukwa chake ndidzakuyamikani pakati pa anthu a mitundu ina, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.” Akutinso, “Inu anthu a mitundu ina, kondwani pamodzi ndi anthu ake a Mulungu.” Ndiponso akuti, “Inu nonse a mitundu ina, tamandani Ambuye, anthu a mitundu yonse amtamande.” Nayenso mneneri Yesaya akuti, “Mmodzi mwa zidzukulu za Yese adzabwera. Iye adzadzambatuka kuti alamule anthu a mitundu ina, ndipo iwo adzaika chikhulupiriro chao pa Iyeyo.” Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Abale anga, ine mwini wake sindikayika konse kuti ndinu anthu a kufuna kwabwino ndithu, ndinu anthu odziŵa zinthu, ndipo mumatha kulangizana. Komabe m'kalata ino zina ndakulemberani mopanda mantha konse, kuti ndikukumbutseni zimenezo. Ndalemba motere popeza kuti Mulungu adandikomera mtima pakundipatula kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu a mitundu ina. Adandipatsa ntchito yolalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu ngati wansembe, kuti anthuwo akhale ngati nsembe yokomera Iye ndi yoperekedwa mwa Mzimu Woyera. Tsono pokhala ndine wake wa Khristu Yesu, ndikunyadira ntchito imene ndikugwirira Mulungu. Sindidzalimba mtima kulankhula za kanthu kena ai, koma zokhazo zimene ndimachita kudzera mwa Khristu, kuti ndithandize anthu a mitundu ina kumvera. Zimenezi ndidazichita ndi mau anga ndi ntchito zanga, ndi zizindikiro ndi zozizwitsa zamphamvu zochitika ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Motero Uthenga Wabwino wonena za Khristu ndidaulalika kwathunthu ku Yerusalemu ndi ku dziko lozungulira mpaka ku Iliriko. Masiku onse ndinkayesetsa kulalika Uthenga Wabwino kumalo kokhako kumene dzina la Khristu linali lisanamvekebe. Ndinkaopa kumanga pa maziko amene munthu wina adaika. Paja Malembo akuti “Anthu amene sadauzidwe za Iye, adzaona, amene sadamve za Iye, adzamvetsa.” Pa chifukwa chimenechi ndidalephera kaŵirikaŵiri kufika kwanuko. Zaka zambiri ndakhala ndikulakalaka kuti ndifike kumeneko. Ndipo tsopano, popeza kuti ndatsiriza ntchito yanga ku mbali zakuno, ndikuyembekeza kudzakuwonani pamene ndidzadzera kwanuko popita ku Spaniya. Ndidzakondwera kukuchezerani masiku angapo, ndipo pambuyo pake ndifuna kuti mudzandithandize kupitiriza ulendo wanga. Koma tsopanoli ndikupita ku Yerusalemu kukapereka chithandizo kwa anthu a Mulungu kumeneko. Pakuti mipingo ya ku Masedoniya, ndi ya ku Akaiya idakoma mtima mpaka kupereka zothandiza osauka pakati pa anthu a Mulungu a ku Yerusalemu. Inde unali ufulu kuchita zimenezi, komanso unali udindo wao kuthandiza osaukawo. Ayuda adagaŵana madalitso ao achikhristu ndi anthu a mitundu ina, choncho iwowo ayeneranso kuthandiza Ayudawo pa zosoŵa zao za moyo wathupi. Tsono nditatsiriza ntchito yangayi, ndi kutula bwino lomwe kwa iwo zoperekazi, ndidzadzera kwanuko popita ku Spaniya. Ndikudziŵa kuti ndikadzabwera kumeneko, ndidzabwera ndi madalitso ochuluka a Khristu. Tsono ndikukupemphani abale, kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu, ndiponso ndi chithandizo cha chikondi chimene Mzimu Woyera amapereka, kuti mugwirizane nane polimbikira kundipempherera kwa Mulungu. Mundipempherere kuti Mulungu anditchinjirize, ndisagwe m'manja mwa anthu osakhulupirira am'Yudeya. Mupempherenso kuti anthu a Mulungu a ku Yerusalemu azilandire ndi manja aŵiri zoperekazi zimene ndatumidwa kuti ndikaŵapatse. Choncho, Mulungu akalola, ndidzafika kwanuko ndili wokondwa, ndipo ndidzasanguluka pocheza nanu. Mulungu amene amapatsa mtendere akhale ndi inu nonse. Amen. Ndikupereka m'manja mwanu Febe, mlongo wathu, amene ali mtumiki wa mpingo wa ku Kenkrea. Mlandireni m'dzina la Ambuye, monga momwe anthu a Mulungu ayenera kulandirirana. Mumthandize monga momwe angasoŵere chithandizo chanu, pakuti iyeyo adathandiza anthu ambiri, ine ndemwenso adandithandizako. Mundiperekere moni kwa Prisika ndi Akwila, anzanga otumikira Khristu Yesu. Iwoŵa anali okonzeka kuphedwa kuti apulumutse moyo wanga. Si ndine ndekhatu ndikuŵathokoza, komanso mipingo yonse ya ku maiko a anthu a mitundu ina. Mundiperekerenso moni kwa anthu amene amasonkhana ngati ampingo m'nyumba mwao. Moni kwa Epeneto, bwenzi langa lapamtima, amene ndi woyamba mu Asiya kukhulupirira Khristu. Moni kwa Maria, amene wakhala akukugwirirani ntchito kolimba. Moni kwa Androniko ndi Yunia, Ayuda anzanga amene anali nane m'ndende. Iwoŵa ndi otchuka pakati pa atumwi, ndipo ndi ine ndi iwowo adayambira ndiwo kukhala akhristu. Moni kwa Ampiliato, bwenzi langa lokondedwa mwa Ambuye. Moni kwa Urbano, mtumiki mnzathu pa ntchito ya Khristu, ndiponso kwa Stakisi, amene ndimamkonda. Moni kwa Apelesi, mkhristu wolimba uja. Moni kwa a m'banja la Aristobulo. Moni kwa Herodiono, Myuda mnzanga. Moni kwa akhristu a m'banja la Narkiso. Moni kwa Trifena ndi Trifosa, amene amagwira mwamphamvu ntchito ya Ambuye. Moni kwa Perisi, wokondedwa uja, amene wachita zambiri pogwirira Ambuye ntchito. Moni kwa Rufu, wotchuka pa ntchito ya Ambuye. Moninso kwa mai wake amene ali ngati mai wanganso. Moni kwa Asinkrito, Filegoni, Heremesi, Patrobasi, Herimasi ndi abale onse amene ali nawo pamodzi. Moni kwa Filologo ndi Juliya, kwa Nereo ndi mlongo wake, kwa Olimpasi ndi kwa anthu onse a Mulungu amene ali nawo pamodzi. Mupatsane moni mwa chikondi choona. Mipingo yonse yachikhristu ikukupatsani moni. Ndikukupemphani abale, chenjera nawoni anthu amene amapatutsa anzao naŵachimwitsa. Iwo amaphunzitsa zosiyana ndi zimene inu mudaphunzira. Muziŵalewa, pakuti anthu otere satumikira Khristu Ambuye athu, koma amangotumikira zilakolako zao basi. Ndi mau okoma ndi oshashalika amanyenga anthu a mitima yoona. Anthu onse adaimva mbiri ya kumvera kwanu. Tsono ine ndikunyadira inuyo, koma ndifuna kuti mukhale anzeru pa zabwino, ndi othaŵa zoipa. Ndipo Mulungu amene amapatsa mtendere, posachedwa adzatswanya Satana pansi pa mapazi anu. Ambuye athu Yesu Khristu akudalitseni. Timoteo, mnzanga wogwira naye ntchito, akukupatsani moni. Lusio, Yasoni ndi Sosipatere, Ayuda anzanga, nawonso akuti moni. Ine Tersio, mlembi chabe wa kalatayi, ndikuti moni, inu abale mwa Ambuye. Akukupatsani moni Gayo, amene akundisamala ine pamodzi ndi mpingo wonse kunyumba kwake. Akukupatsani moni Erasito, msungachuma wa mzinda wonse, ndiponso Kwarto, mbale wathu. [ Ambuye athu Yesu Khristu akudalitseni nonse. Amen.] Tiyeni tilemekeze Mulungu! Iye ali ndi mphamvu za kukulimbitsani potsata Uthenga Wabwino umene ndimaulalika, umene ndi mau olengeza za Yesu Khristu. Zimenezi zinali zachinsinsi, ndipo zidaabisika pa zaka zonse kuyambira kalekale. Koma tsopano zatulukira poyera kudzera m'zimene aneneri adalemba, ndiponso kudzera m'lamulo la Mulungu wachikhalire zadziŵika kwa anthu a mitundu yonse, kuti azizikhulupirira ndi kuzimvera. Kwa Mulungu, amene ndiye yekha wanzeru, kukhale ulemerero mwa Yesu Khristu mpaka muyaya. Amen. Ndine, Paulo, amene mwa kufuna kwa Mulungu ndidaitanidwa kuti ndikhale mtumwi wa Khristu Yesu. Ndili pamodzi ndi mbale wathu, Sostene. Tikulembera mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto. Mulungu adakupatulani mwa Khristu Yesu, ndipo adakuitanani kuti mukhale anthu akeake, pamodzi ndi anthu onse amene ponseponse amatama dzina la Ambuye Yesu Khristu mopemba. Iye ndiye Mbuye wathu ndi Mbuye waonso. Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere. Nthaŵi zonse ndimayamika Mulungu wanga chifukwa cha inu, popeza kuti adakukomerani mtima mwa Khristu Yesu. Zoonadi mwa Khristu mwakhala anthu olemera pa zonse, makamaka pa kulankhula ndi pa kudziŵa zinthu, popeza kuti mau ochitira Khristu umboni akhazikika mwa inu. Nchifukwa chake palibe mphatso yauzimu imene yakupereŵerani, pamene mukudikira kubweranso kwa Ambuye athu Yesu Khristu. Iye adzakulimbitsani mpaka chimalizo, kuti mudzakhale opanda cholakwa pa tsiku la Ambuye athu Yesu Khristu. Mulungu ndi wokhulupirika, ndipo Iye ndiye amene adakuitanani kuti mukhale a mtima umodzi ndi Mwana wake Yesu Khristu Ambuye athu. Abale, ndikukupemphani m'dzina la Ambuye athu Yesu Khristu, kuti muzivomerezana pa zimene munena. Pasakhale kupatulana pakati panu, koma muzimvana kwenikweni pokhala a mtima umodzi ndi a maganizo amodzi. Pakuti ena a m'banja la Koloe andifotokozera kuti pali kukangana pakati panu, abale anga. Chimene ndikufuna kunena nchakuti aliyense mwa inu akungonena zakezake. Wina akuti, “Ine ndine wa Paulo,” winanso akuti, “Ine ndine wa Apolo,” wina akuti, “Ine ndine wa Kefa,” winanso akuti, “Ine ndine wa Khristu.” Kodi Khristu wagaŵika? Kodi adakuferani pa mtanda ndi Paulo? Kodi mudabatizidwa m'dzina la Paulo? Ndimayamika Mulungu kuti pakati panupo sindidabatize wina aliyense, kupatula Krispo ndi Gayo basi. Motero palibe amene anganene kuti adabatizidwa m'dzina langa. Inde ndidabatizanso Stefanasi ndi a m'banja mwake, koma sindikumbukira kuti pali winanso amene ndidamubatiza. Paja Khristu adandituma, osati kuti ndizibatiza ai, koma kuti ndizilalika Uthenga Wabwino. Ndipo ndiyenera kumaulalika mosagwiritsa ntchito luso lake la ulaliki, kuwopa kuti mtanda wa Khristu ungatheretu mphamvu. Mau onena za imfa ya Khristu pa mtanda ndi chinthu chopusa kwa anthu amene akutayika, koma kwa ife amene tili pa njira ya chipulumutso, mauwo ndi mphamvu ya Mulungu. Paja Malembo akuti, “Ndidzaononga nzeru za anthu anzeru, ndidzathetsa kuchenjera kwa anthu ochenjera.” Nanga ali kuti anthu anzeru? Ali kuti aphunzitsi a Malamulo a Mose? Ali kuti anthu onyadira nzeru zamakono zapansipano? Monga Mulungu sadaonetse kuti kudalira nzeru zapansipano nkopusa? Pakuti mwa nzeru zake Mulungu adakonzeratu kuti anthuwo asamdziŵe ndi nzeru zao. Koma kudamkomera Mulungu kupulumutsa anthu okhulupirira ndi mau opusa amene timalalika. Ayuda amafuna kuwona zozizwitsa, pamene Agriki amafunafuna nzeru. Koma ife timalalika Khristu amene adapachikidwa pa mtanda. Kwa Ayuda mau ameneŵa ndi okhumudwitsa, pamene kwa anthu a mitundu ina mauŵa ndi opusa. Koma amene Mulungu adaŵaitana, kaya ndi Ayuda kaya ndi Agriki, onsewo amazindikira kuti Khristu ndi mphamvu ya Mulungu ndiponso nzeru ya Mulungu. Pajatu chimene chimaoneka ngati kupusa kwa Mulungu, nchanzeru kupambana nzeru za anthu. Ndipo chimene chimaoneka ngati kufooka kwa Mulungu, nchamphamvu kupambana mphamvu za anthu. Abale, taganizani m'mene munaliri pamene Mulungu adakuitanani. Pakati panu panalibe ambiri amene anthu ankaŵayesa anzeru. Panalibenso ambiri amphamvu, kapena obadwa m'mabanja omveka. Koma Mulungu adasankha zimene anthu amaziyesa zopusa, kuti Iye anyazitse nazo anthu anzeru. Adasankhanso zimene anthu amaziyesa zofooka, kuti Iye anyazitse nazo anthu amphamvu. Ndipo zimene anthu amaziyesa zachabe, zonyozeka ndi zosakhala zenizeni, Mulungu adazisankha kuti athetse mphamvu zinthu zimene iwowo amayesa kuti ndiye zenizeni. Mulungu adachita zimenezi kuti pasakhale wina aliyense woti nkumadzitukumula pamaso pake. Mulungu ndiye adakulunzanitsani ndi Khristu Yesu, ndipo adamsandutsa kuti akhale nzeru yathu. Chifukwa cha Yesu, timapezeka olungama pamaso pa Mulungu. Ndi Yesuyo amene amatisandutsa anthu akeake a Mulungu, ndiye amatipulumutsa. Nchifukwa chake, monga Malembo anenera, “Wofuna kunyada, anyadire Ambuye.” Abale, inetu pamene ndidafika kwanu kuti ndikulalikireni chinsinsi chimene Mulungu adatiwululira, sindidayese kulankhula mwaluso, ngati munthu wodziŵa zapatali. Koma ndidaatsimikiza kuti pamene ndili pakati panu, ndiiŵale zina zonse, kupatula Yesu Khristu yekha, koma tsono amene adapachikidwa pa mtanda. Choncho pamene ndidafika kwanuko, ndinali wofooka, ndiponso ndinkanjenjemera kwambiri ndi mantha. Ndipo pamene ndinkalankhula kapena kulalika, sindinkalankhula moonetsa nzeru, kuyesa kukopa anthu, koma mau anga anali otsimikizika ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Ndinkachita zimenezi kuti chikhulupiriro chanu chisakhazikike pa nzeru za anthu, koma chikhazikike pa mphamvu za Mulungu. Komabe pakati pa anthu okhwima m'chikhulupiriro, timalankhula zanzeru. Koma nzeruzo si za masiku anozi, kapena za akulu olamulira dziko lino lapansi, amene mphamvu zao nzodzatha. Nzeru zimene timalankhula, ndi nzeru za Mulungu, zachinsinsi, zobisika kwa anthu. Mulungu asanalenge dziko lapansi, adaakonzeratu zimenezi kuti atipatse ulemerero. Panalibiretu wolamulira wa masiku ano wodziŵa zimenezi. Akadazidziŵa, sakadapachika Ambuye aulemerero pa mtanda. Koma ndi monga Malembo anenera kuti, “Maso a munthu sanaziwone, makutu a munthu sanazimve, mtima wa munthu sunaganizepo konse zimene Mulungu adaŵakonzera amene amamkonda.” Ifeyo Mulungu adatiwululira zimenezi mwa Mzimu Woyera. Pajatu Mzimuyo amadziŵa zinthu zonse kotheratu, ngakhalenso maganizo ozama a Mulungu. Kodi za munthu angazidziŵe ndani, osakhala mzimu wa mwiniwake yemweyo umene uli mwa iyeyo? Momwemonso palibe munthu amene angadziŵe za Mulungu, koma Mzimu wa Mulungu Mwini. Ife sitidalandire mzimu wa dziko lino lapansi, koma tidalandira Mzimu Woyera wochokera kwa Mulungu, kuti adzatithandize kumvetsa zimene Mulunguyo adatipatsa mwaulere. Timalankhula zimenezi osati ndi mau ophunzitsidwa ndi nzeru za anthu, koma ndi mau amene Mzimu Woyera amatiphunzitsa. Timaphunzitsa zoona zauzimu kwa anthu amene ali naye Mzimu Woyera. Munthu wodalira nzeru zake zokha sangalandire zimene zimachokera kwa Mzimu wa Mulungu. Amaziyesa zopusa, ndipo sangathe kuzimvetsa, popeza kuti zimalira kukhala ndi Mzimu Woyera kuti munthu azimvetse. Munthu amene ali ndi Mzimu Woyera angathe kuzindikira khalidwe la zonse, ndipo palibe wina amene angathe kutsutsapo ai. Ndi monga Malembo anenera kuti, “Ndani adadziŵa maganizo a Ambuye, kuti athe kuŵalangiza?” Koma ife tili ndi maganizo a Khristu. Tsono ine, abale, sindidathe kulankhula nanu monga momwe ndimalankhulira ndi anthu amene ali ndi Mzimu Woyera. Koma ndidaayenera kulankhula nanu ngati anthu odalira zapansipano, kapenanso ngati ana akhanda m'moyo wanu wachikhristu. Ndidakumwetsani mkaka, osakupatsani chakudya cholimba, chifukwa simukadatha kuchidya. Ngakhalenso tsopano simungathe kuchidya, popeza kuti mukudalirabe zapansipano. Pakati panu pali kaduka ndi kukangana. Nanga zimenezi sizikutsimikiza kuti mukudalirabe zapansipano, ndipo kuti mumachita monga momwe amachitira anthu odalira zapansipanozo? Mumangoti ali apa, “Ine ndine wa Paulo,” ali apa, “Ine ndine wa Apolo.” Kodi mukamatero simukuchita ngati anthu odalira zapansipano? Kodi Apolo nchiyani? Paulonso nchiyani? Ndi atumiki chabe a Mulungu, amene adakufikitsani ku chikhulupiriro. Aliyense adangogwira ntchito imene Mulungu adampatsa. Ineyo ndidabzala mbeu, Apolo nkuzithirira, koma amene adazimeretsa ndi Mulungu. Motero wobzala kapenanso wothirira sali kanthu, koma Mulungu yekha amene amameretsa, ndiye ali kanthu. Tsono wobzala sasiyana ndi wothirira, ndipo aliyense adzalandira mphotho yake molingana ndi ntchito imene adaigwira. Komabe ife ndife okhaokha ogwira ntchito ya Mulungu, inuyo ndinu munda wa Mulungu, ndinunso nyumba ya Mulungu. Popeza kuti Mulungu adachita kundituma, ndidakhazika maziko monga mmsiri waluso, ndipo wina akumanga pa mazikowo. Koma aliyense azichenjera pomanga. Pajatu palibe maziko enanso amene wina aliyense angathe kukhazika osiyana ndi maziko amene alipo kale. Mazikowo ndi Yesu Khristu. Pa mazikoŵa munthu angathe kumangapo ndi golide, siliva, miyala yamtengowapali, mitengo, udzu kapena mapesi. Koma ntchito za munthu aliyense zidzaonekera poyera, pamene tsiku la chiweruzo lidzaziwonetsa. Pakuti tsikulo lidzafika ndi moto, ndipo motowo ndi umene udzayesa ntchito za munthu aliyense. Zimene munthu adamanga pamazikopo zikadzakhalapobe, mwiniwakeyo adzalandira mphotho. Koma zikadzanyeka ndi moto, sadzalandira mphotho. Inde mwiniwakeyo adzapulumukabe, koma monga ngati munthu amene wangopulumuka m'moto. Kodi inu simudziŵa kuti ndinu nyumba ya Mulungu ndipo kuti Mzimu wa Mulungu amakhala mwa inu? Ngati wina aliyense aononga nyumba ya Mulunguyo, Mulungu nayenso adzamuwononga ameneyo. Pakuti nyumba ya Mulungu ndi yopatulika, ndipo nyumbayo ndinu amene. Tsono musadzinyenge. Ngati wina mwa inu adziyesa wanzeru, kunena za nzeru za masiku ano, ameneyo ayambe wakhala ngati wopusa, kuti asanduke wanzeru. Zoonadi nzeru za anthu odalira zapansipano, nzopusa pamaso pa Mulungu. Pajatu Malembo akuti, “Mulungu amakola anthu anzeru m'kuchenjera kwao.” Penanso Malembo akuti, “Ambuye amaŵadziŵa maganizo a anthu anzeru kuti ndi achabe.” Nchifukwa chake pasakhale wina aliyense wonyadira anthu chabe. Zinthu zonse nzanu: Paulo, Apolo ndi Kefa, dziko lapansi, moyo ndi imfa, zimene zilipo ndi zimene zilikudza. Koma ngakhale zonsezi nzanu, inu ndinu ake a Khristu, ndipo Khristu ndi wake wa Mulungu. Muzitiwona ngati antchito a Khristu, ngati akapitao osamala zinsinsi za Mulungu. Chofunika chachikulu pa akapitao otere nchakuti akhale okhulupirika. Kunena za ine ndekha, ndilibe nazo kanthu ngati ndiweruzidwa ndi inu, kapenanso ndi bwalo lina lililonse la anthu. Ndiponsotu ngakhale mwiniwakene sindidziweruza ndekha ai. Ndilibe kanthu konditsutsa mumtima mwanga, komabe ngakhale chimenechi si chitsimikizo chakuti ndine wolungama. Ondiweruza ndi Ambuye basi. Motero musaweruziretu munthu aliyense, Ambuye asanabwere. Iwo ndiwo adzaunika pa zonse zobisika mu mdima, ndipo adzaulula maganizo a m'mitima mwa anthu. Pamenepo aliyense adzalandira kwa Mulungu chiyamiko chomuyenerera. Abale, zimene ndanenazi nzokhudza ine ndi Apolo. Ndifuna kuti zimenezi zikuphunzitseni tanthauzo la mau aja akuti, “Musapitirire zimene Malembo akunena.” Nchifukwa chake musamanyadira wina, ndi kupeputsa mnzake. Nanga adakusiyanitsa ndi anthu ena ndani? Kaya uli ndi chiyaninso chimene sudachite kuchilandira? Tsono ngati udachita kuzilandira, ukunyadiranji ngati kuti sudangozilandira chabe? Ndiye kuti muli nazo kale zonse zimene mumasoŵa! Ndiye kuti mwalemera kale! Ndiye kuti mwasanduka mafumu popanda ife! Ndikadakondwera mukadakhaladi mafumu, kuti ifenso tikhale mafumu pamodzi nanu. Ndikuwona kuti atumwife Mulungu adatipatsa malo a kuthungo kwenikweni, ngati anthu oti akukaphedwa. Ndithu tasanduka ngati chinthu chochiwonetsa kwa zolengedwa zonse, osati anthu okha ai, komanso ndi angelo omwe. Ife ndife opusa chifukwa cha Khristu, koma inu ndinu anzeru mwa Khristu. Ife ndife ofooka, koma inu ndinu amphamvu. Inu mumalandira ulemu, koma ife timanyozedwa. Mpaka tsopano lino timamva njala ndi ludzu, ndipo ndife ausiŵa. Anthu akutimenya, ndipo tilibe pokhala penipeni. Tikugwira ntchito kolimba ndi manja athu kuti tidzisunge. Anthu akamatichita chipongwe, timapempha kuti Mulungu aŵadalitse. Anthu akamatizunza, timangopirira. Anthu akamatilalatira, timangoŵayankha moleza. Tasanduka onyozeka, ngati zinyatsi za dziko lapansi, ndipo mpaka tsopano anthu onse akutiyesa zinyalala. Ndikukulemberani zonsezi, osati kuti ndikuchititseni manyazi, koma kuti ndikulangizeni, chifukwa ndinu ana anga okondedwa. Ngakhale mutakhala nawo aphunzitsi ambirimbiri m'moyo wanu wachikhristu, simukhala ndi atate ambiri ai. Pajatu m'moyo wanu wachikhristu ine ndidachita ngati kukubalani pakukulalikirani Uthenga Wabwino. Ndikukupemphani tsono kuti muzinditsanzira. Nchifukwa chake ndakutumizirani Timoteo, mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye. Iyeyu adzakukumbutsani za mayendedwe anga achikhristu, amene sasiyana ndi zimene ndimaphunzitsa ponseponse m'mipingo yonse. Ena mwayamba kudzitukumula, monga ngati sindidzabwerako kwanu. Koma Ambuye akalola, ndidzabwera kwanuko posachedwa. Pamenepo ndidzadziŵa zimene odzitukumulawo angathe kuchita, osati zimene amangonena chabe. Pakuti mu Ufumu wa Mulungu chachikulu si mau chabe, koma ntchito. Nanga mukufuna chiyani? Mukufuna kuti ndidzabwere kwanuko ndi mkwapulo, kapena ndi mtima wachikondi ndi wofatsa? Mbiri yawanda ponseponse yonena kuti pakati panu pali dama. Ndipo damalo ndi la mtundu wakuti ndi anthu akunja omwe sachita. Ndamva ndithu kuti munthu wina akukhala ndi mkazi wa bambo wake. Ndipo inu mukudzitukumulabe! Kwenikweni mukadayenera kumva chisoni, ndi kumchotsa pakati panu munthu amene adachita zimeneziyo. Kunena za ine, ngakhale sindili nanu pamodzi, komabe mtima wanga uli nanu ndithu. Mwakuti ndamuweruza kale munthu amene adachita zimeneziyo, monga ngati ndili nanu pamodzi. Tsono mutasonkhana m'dzina la Ambuye Yesu, inenso m'maganizo ndili nanu pomwepo, ndi mphamvu ya Ambuye athu Yesu, munthuyo mumpereke kwa Satana, kuti thupi lake liwonongedwe, ndipo pakutero mzimu wake udzapulumutsidwe pa tsiku la Ambuye. Pamenepo palibe choti inu nkunyadira ai. Kodi simuŵadziŵa mau aja akuti, “Chofufumitsira buledi chapang'ono chimafufumitsa mkate wonse?” Muchotse chofufumitsira chakalechi cha uchimo, kuti mukhale oyera mtima ndithu, ngati buledi watsopano wosafufumitsa, monga momwe muliri ndithu, pakuti Khristu, Mwanawankhosa wathu wa Paska, adaphedwa kale ngati nsembe. Tiyeni tsono, tichite chikondwererocho, osati ndi chofufumitsira chakale chija cha uchimo ndi cha kuipa mtima, koma ndi buledi wosafufumitsa, wa kuyera mtima ndi wa choona. M'kalata imene ndidaakulemberani, ndidaakuuzani kuti musamayanjane nawo anthu adama. Sindiye kuti muziŵapewa anthu onse apansipano amene ali adama, aumbombo, achifwamba, kapena opembedza mafano ai. Kuti mutero kukadafunika kuti mungochokamo m'dziko lino lapansi. Koma ndidaakulemberani kuti musamayanjane ndi munthu amene amati ndi mkhristu, pamene chikhalirecho ndi munthu wadama, kapena waumbombo, wopembedza mafano, waugogodi, chidakwa, kapena wachifwamba. Munthu wotere musamadye naye nkomwe. Nanga kuweruza anthu amene adakali kunja, ndi ntchito yanga ngati? Si koma amene ali mu mpingo ndiwo muyenera kuŵaweruza? Ndi Mulungu amene amaweruza anthu akunjawo. Paja mau a Mulungu akuti, “Munthu woipayo mumchotse pakati panu.” Ngati wina ali ndi mlandu ndi mkhristu mnzake, angathe bwanji kukauzengetsa kwa oweruza amene ali akunja, osati kwa akhristu anzake? Kodi simukudziŵa kuti akhristu ndiwo adzaweruza anthu onse? Tsono ngati inu mudzaweruza anthu onse, kodi simungathe kuweruza ngakhale ndi timilandu tating'ono tomwe? Kodi simukudziŵa kuti tidzaweruza angelo? Nanji zinthu za moyo wapansipano? Tsono ngati muli ndi milandu pa zinthu zotere, bwanji mumaika anthu amene mpingo suŵayesa kanthu kuti aiweruze? Ndikunena zimenezi kuti ndikuchititseni manyazi. Kodi mwa inu palibe ndi mmodzi yemwe wanzeru, amene angathe kuweruza mlandu pakati pa akhristu anzake? Bwanji mkhristu akuimba mlandu mkhristu mnzake, mlanduwo nkuupereka kwa anthu akunja kuti auzenge? Chokha chakuti mumaimbana milandu inu nokhanokha, chatsimikiza kale kuti mwalephereratu. Bwanji osangopirira pamene ena akulakwirani? Bwanji osangolola kuti inuyo akubereni? Koma inuyo ndi amene mukulakwira ena, ndipo mukuŵabera, ngakhale iwowo ndi akhristu anzanu! Kani simudziŵa kuti anthu osalungama sadzaulaŵa Ufumu wa Mulungu? Musadzinyenge: anthu adama, opembedza mafano, achigololo, ochimwa ndi amuna anzao, mbala, aumbombo, zidakwa, augogodi, kapena achifwamba, ameneŵa sadzaulaŵa Ufumu wa Mulungu. Enanu munali otere kale, koma mudayeretsedwa, mudasanduka anthu a Mulungu, ndipo mudapezeka olungama pamaso pake. Zimenezi zidachitika m'dzina la Ambuye Yesu Khristu, ndiponso mwa Mzimu wa Mulungu wathu. Zinthu zonse nzololedwa kwa ine, koma si zonse zili ndi phindu. Zonse nzololedwadi kwa ine, koma sindingalole kuti chilichonse chindigonjetse. Chakudya, kwake nkuloŵa m'mimba, ndipo mimba, kwake nkulandira chakudya. Koma Mulungu adzaononga ziŵiri zonsezo. Thupi la munthu si lochitira dama, koma ndi la Ambuye, ndipo Ambuye ndiwo mwiniwake thupilo. Mulungu adaukitsa Ambuye kwa akufa, ndipo mwa mphamvu yake adzatiwukitsa ifenso. Kodi inu simudziŵa kuti matupi anu ndi ziwalo za Khristu? Monga tsono ine nkutenga ziwalo za Khristu nkuzisandutsa ziwalo za mkazi wadama? Chosatheka! Kaya simudziŵa kuti munthu amene amadzipereka kwa mkazi wadama, iyeyo ndi mkaziyo amasanduka thupi limodzi? Paja Malembo akuti, “Aŵiriwo adzasanduka thupi limodzi.” Koma amene amadzipereka kwa Ambuye, iyeyo ndi Ambuye amakhala mzimu umodzi. Thaŵani dama. Tchimo lina lililonse limene munthu amachita, siliipitsa thupi lake, koma munthu wadama amachimwira thupi lake lomwe. Kodi simudziŵa kuti thupi lanu ndi nyumba ya Mzimu Woyera? Mulungu adakupatsani Mzimuyo kuti akhale mwa inu. Nchifukwa chake moyo umene muli nawo si wanunso. Mulungu adakugulani ndi mtengo wapatali, tsono muzimlemekeza ndi matupi anu. Tsopano ndiyankhe zimene mudandifunsa m'kalata yanu. Nkwabwino kuti munthu asakwatire, koma kuwopa dama, mwamuna aliyense akhale ndi mkazi wakewake, ndipo mkazi aliyense akhale ndi mwamuna wakewake. Mwamuna azipereka kwa mkazi wake zomuyenerera zokhudza banja ngati mkazi wake, momwemonso mkazi azipereka kwa mwamuna wake zomuyenerera zokhudza banja ngati mwamuna wake. Mkazi thupi lake si lokhalira iye yekha ai, ndi lokhaliranso ndi mwamuna wake yemwe. Momwemonso mwamuna thupi lake si lokhalira iye yekha ai, ndi lokhaliranso ndi mkazi wake yemwe. Musamakanane, koma pokhapokha mutavomerezana kutero pa kanthaŵi kuti mudzipereke ku mapemphero. Pambuyo pake mukhalenso pamodzi, kuwopa kuti Satana angakuyeseni chifukwa cha kulephera kudzigwira. Pamene ndikunena zimenezi, sindikuchita mokulamulani ai, koma mokulolani chabe. Kwenikweni ndikadakonda kuti anthu onse akhale ngati ine, koma Mulungu adapatsa munthu aliyense mphatso yakeyake, wina mphatso yakuti, winanso yakuti. Kwa amene sali pa banja, ndiponso kwa azimai amasiye, mau anga ndi aŵa: Nkwabwino kuti iwo akhalebe paokha choncho ngati ineyo. Koma ngati sangathe kudziletsa, aloŵe m'banja, pakuti nkwabwino kuloŵa m'banja kupambana kupsa ndi moto wa zilakolako. Kwa anthu am'banja lamulo langa, limenetu kwenikweni ndi lochokera kwa Ambuye, ndi ili: Mkazi asalekane ndi mwamuna wake. Koma ngati amuleka, akhale wosakwatiwanso, kapena ayanjane nayenso mwamuna wakeyo. Chimodzimodzinso mwamuna asasudzule mkazi wake. Kwa ena mau anga, osati a Ambuye ai, ndi aŵa: Ngati mkhristu ali ndi mkazi wachikunja, ndipo mkaziyo avomera kukhala naye, mwamunayo asathetse ukwatiwo. Momwemonso ngati mkhristu wamkazi ali ndi mwamuna wachikunja, ndipo mwamunayo avomera kukhala naye, mkaziyo asathetse ukwatiwo. Pakuti mwamuna wachikunja uja amadalitsidwa chifukwa cha mkazi wakeyo. Nayenso mkazi wachikunja uja amadalitsidwa chifukwa cha mwamuna wakeyo. Pakadapanda apo, bwenzi ana anu atakhala akunja, koma monga zilirimu, ndi ana a Mulungu. Koma ngati wakunja uja afuna kuleka mkhristu, amuleke. Zikatero, ndiye kuti mkhristu wamwamunayo kapena wamkaziyo ali ndi ufulu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale ndi moyo wamtendere. Kodi iwe, mkazi wachikhristu, ungadziŵe bwanji ngati udzampulumutsa mwamuna wako? Kapenanso iwe, mwamuna wachikhristu, ungadziŵe bwanji ngati udzapulumutsa mkazi wako? Aliyense atsate moyo umene Ambuye adamkonzera, moyo umene Mulungu adamuitanira. Ndizo zimene ndimaŵalamula anthu onse amumpingo. Ngati wina Mulungu adamuitana ali woumbalidwa, asavutike nkubisa kuumbala kwakeko. Chimodzimodzi ngati wina adamuitana ali wosaumbalidwa, asaumbalidwe. Kuumbala si kanthu ai, kusaumbala si kanthunso. Kanthu nkutsata malamulo a Mulungu. Aliyense angokhala monga momwe analiri pamene Mulungu adamuitana. Kodi unali kapolo pamene Mulungu adakuitana? Usavutike nazo. Komanso ngati upeza mwai woti ulandire ufulu, uugwiritse ntchito mwaiwo. Pakuti munthu amene anali kapolo pamene Ambuye adamuitana, ameneyo ndi mfulu ya Ambuye. Momwemonso amene anali mfulu pamene Ambuye adamuitana, ameneyo ndi kapolo wa Khristu. Mulungu adakugulani ndi mtengo wapatali, tsono musasanduke akapolo a anthu. Abale, aliyense angokhala pamaso pa Mulungu monga momwe analiri pamene Mulunguyo adamuitana. Kunena za amene sali pa banja, ndilibe lamulo lochokera kwa Ambuye. Koma ndikuuzani maganizo anga, ngati munthu amene Ambuye adandichitira chifundo kuti ndikhale wokhulupirika. Chifukwa cha masautso a nthaŵi ino, ndiyesa nkwabwino kuti munthu akhale monga momwe aliri. Kodi ndiwe wapabanja? Usayese kuthetsa banja lako. Kodi ndiwe wopanda banja? Usayese kupeza banja. Komabe ngati ukwatira, sukuchimwa ai. Ndipo ngati namwali akwatiwa, sakuchimwa ai. Komabe oloŵa m'banja adzakumana ndi zovuta m'moyo wao, ndipo pano ndingofuna kukupewetsani zovutazo. Chimene ndikukuuzani, abale, nchakuti nthaŵi yachepa. Kuyambira tsopano anthu okwatira akhale monga ngati sadakwatire. Amene akulira, akhale monga ngati sakulira, amene akukondwa, akhale monga ngati sakukondwa, amene akugula zinthu, akhale monga ngati sali nazo zinthuzo. Ndipo amene akugwiritsa ntchito zinthu zapansipano, zisaŵagwire mtima zinthuzo. Pakuti dziko lino lapansi, monga liliri tsopanomu, likupita. Ndidakakonda kuti pasakhale zokudetsani nkhaŵa. Munthu wosakwatira amangotekeseka ndi za Ambuye, kuganiza za m'mene angakondweretsere Ambuye. Koma munthu wokwatira amatekeseka ndi zapansipano, kuganiza za m'mene angakondweretsere mkazi wake. Motero amagwira njakata. Mkazi wosakwatiwa, kapenanso namwali, amangotekeseka ndi za Ambuye, kuti adzipereke kwa Ambuye m'thupi ndi mumzimu momwe. Koma mkazi wokwatiwa amatekeseka ndi zapansipano, kuganiza za m'mene angakondweretsere mwamuna wake. Ndikunenatu zimenezi kufuna kuti ndikuthandizeni, osati kuti ndikuletseni ufulu wanu ai. Makamaka ndifuna kuti muzichita zonse moyenera, ndipo kuti muzidzipereka kwathunthu potumikira Ambuye. Koma ngati wina akuganiza kuti akumlakwira namwali wake amene adamtomera, ndipo ngati namwaliyo unamwali wake ukupitirira, tsono munthuyo nkuganiza kuti ayenera kumkwatira, angathe kuchita zimenezo, si kuchimwa ai. Komabe ngati wina, mwaufulu wake, popanda womukakamiza, watsimikiza kwenikweni kuti samkwatira namwali adamtomerayo, nayenso wachita bwino. Ndiye kuti, munthu wokwatira namwali amene adamtomera, akuchita bwino, koma woleka osamkwatira, akuchita bwino koposa. Mkazi amamangika ndi lamulo la ukwati, nthaŵi yonse pamene mwamuna wake ali moyo. Koma mwamuna wake akamwalira, ali ndi ufulu kukwatiwa ndi mwamuna amene iye afuna, malinga ukwatiwo ukhale wachikhristu. Koma m'mene ndikuganizira ine, adzakhala wokondwa koposa ngati akhala wosakwatiwanso. Ndipo ndikuyesa inenso ndili naye Mzimu wa Mulungu. Tsopano ndifuna kunena za chakudya choperekedwa kwa mafano. Nzoonadi kuti tonse tili nazo nzeru, komatu nzeru zokha zimangotukumula anthu. Chikondi ndicho chimapindulitsa. Munthu amene amadziyesa wodziŵa kanthu, ndiye kuti sakudziŵabe kwenikweni monga momwe akadayenera kudziŵira. Koma munthu akamakonda Mulungu, ndiye kuti amadziŵika ndi Mulungu. Ndinene tsono za chakudya choperekedwa kwa mafano. Tikudziŵa kuti fano si kanthu konse, ndiponso kuti palibe mulungu wina, koma Mulungu mmodzi yekha. Ena amati kuli zinthu zina kumwambaku, kapena pansi pano, zimene iwo amazitchula milungu, ndipo anthuwo ali nayodi milungu yambiri, ndi ambuye ambiri. Koma kwa ife, Mulungu ndi mmodzi yekha, ndiye Atate, amene adalenga zonse, ndipo moyo wathu umalinga kwa Iye. Tilinso ndi Ambuye amodzi okha, Yesu Khristu. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, ndipo ife tili ndi moyo chifukwa cha Iye. Komabe si onse amene amadziŵa zimenezi. Ena adazoloŵera kupembedza mafano, ndipo mpaka lero akamadya chakudya choperekedwa kwa mafano, amaganiza ndithu kuti chakudyacho chidaperekedwadi kwa mafano. Tsono popeza kuti ali ndi mitima yofooka, mitima yaoyo imaipitsidwa. Nzoona kuti chakudya sichitifikitsa pafupi ndi Mulungu. Tikapanda kudya chakudyacho, sititayapo kanthu, komanso tikachidya, sitipindulapo kanthu. Komabe chenjerani kuti ufulu wanuwu pochita zinthu, ungaphunthwitse ena amene chikhulupiriro chao nchosalimba kwenikweni. Ngati iweyo amene uli wodziŵa udya m'nyumba yopembedzeramo fano, nanga tsono munthu wosadziŵa kwenikweni, atakuwona ukuchita zimenezi, kodi chimenechi sichidzamlimbitsa mtima kuti nayenso azidya chakudya choperekedwa kwa mafano? Motero amene chikhulupiriro chake nchosalimba kwenikweni, adzatayika chifukwa cha iwe amene uli wodziŵa. Chonsecho tsono iyeyo ndi mbale wako amene Khristu adamufera! Mukamachimwira abale anu achikhristu motero, ndi kulakwitsa amene ali ndi mitima yofooka, mukuchimwiranso ndi Khristu yemwe. Nchifukwa chake, ngati chakudya chingaphunthwitse mbale wanga wachikhristu, sindidzadya konse nyama, kuti ndingamuphunthwitse mbale wangayo. Kodi sindine mfulu? Kodi sindine mtumwi? Kodi suja ine ndidamuwona Yesu Ambuye athu? Kodi suja inu ndinu zipatso za ntchito yanga yogwirira Ambuye? Ngakhaletu ena sandiyesa mtumwi, koma kwa inu ndine mtumwi ndithu, pakuti moyo wanu wachikhristu ndi umboni wakuti ndinedi mtumwi. Zimene ndimaŵayankha ofufuza za ine ndi izi: Kodi si koyenerera kwa ife kumalandira chakudya ndi chakumwa? Kodi si koyenerera kwa ife kuti ŵaakazi azitsagana nafe pa maulendo athu, monga zikuchitikira ndi atumwi ena ngakhalenso abale a Ambuye ndiponso Kefa. Kodi ine ndi Barnabasi, ndife tokha oyenera kugwira ntchito zamanja kuti tizidzipezera tokha zotisoŵa. Kodi alipo msilikali womadzipezera yekha zofunika zonse? Kodi alipo munthu wobzala mpesa, koma osadyako zipatso zake? Kodi alipo munthu wokhala ndi ziŵeto, koma osamwako mkaka wake? Kodi zimene ndikunenazi ndi nzeru za anthu chabe? Suja Malamulo a Mose amanena zomwezi? Paja timaŵerenga m'Malamulowo kuti, “Usaimange pakamwa ng'ombe pamene ikupuntha tirigu.” Kodi pamene adanena zimenezi, Mulungu adangosamala za ng'ombe zokha? Kodi sankanena zimenezi makamaka chifukwa cha ife? Adazilembadi chifukwa cha ife, pakuti wolima ndiponso wopuntha, onsewo amagwira ntchito yao ndi chiyembekezo chakuti nawonso adzalandirako kanthu pa zokolola. Ngati ife tidafesa zabwino zauzimu pakati panu, nanga tilekerenji kulandira kwa inu zotisoŵa m'moyo wathu wathupi? Ngati ena adziyesa kuti ndi oyenera kulandira zimenezi kwa inu, nanga ife sindiye oyenera koposa iwowo kuzilandira? Komabe kuyenera kumeneku sitidakugwiritse ntchito ai. Makamaka tidapirira zonse, kuwopa kuti tingachedwetse anthu mwa njira iliyonse kulandira Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Kodi simudziŵa kuti otumikira m'Nyumba ya Mulungu, amadya chakudya cha m'Nyumbamo, ndipo kuti opereka nsembe pa guwa lansembe, amalandira nao zansembezo? Momwemonso Ambuye adalamula kuti olalika Uthenga Wabwino, azilandira zoŵasunga pakulalika Uthengawo. Koma ineyo sindinkagwiritsa ntchito konse lamulo limeneli. Ndiponso sindikulemba kalatayi chifukwa chofuna kuligwiritsa ntchito kumene. Kwenikweni ndikadakonda kuti ndife, kupambana kuti wina andichotsere chifukwa chimene ndimanyadira. Komabe pamene ndikulalika Uthenga Wabwino, apo pokha palibe ponyadira ai, popeza kuti ndi Ambuye amene adachita kundilamula zimenezo. Tsoka kwa ine ngati sindiulalika Uthenga Wabwinowo. Ngatitu ndikugwira ntchitoyi mofuna ine ndekha, ndiye kuti ndilandirapo mphotho. Koma ngati ndiigwira mosafuna ine ndekha, ndiye kuti ntchitoyo ndi udindo umene Ambuye adandipatsa. Pamenepo tsono mphotho yanga ndi yotani? Mphotho yanga ndi yakuti ndikamalalika Uthenga Wabwino, ndizingoulalika mwaulere, osafuna kulandirapo malipiro aja amene ndikadayenera kulandira polalika Uthenga Wabwinowo. Ndine mfulu, osati kapolo wa munthu wina aliyense ai, komabe ndidadzisandutsa kapolo wa anthu onse, kuti ndikope anthu ambiri. Kwa Ayuda ndidakhala ngati Myuda, kuti ndiŵakope. Ngakhale ineyo sindilamulidwa ndi Malamulo a Mose, komabe kwa Ayuda amene ali olamulidwa ndi Malamulowo, ndidakhala ngati iwo omwe, kuti ndiŵakope. Kwa amene alibe Malamulo a Mose, ndidakhala ngati iwo omwe, kuti ndiŵakope. Sindiye kuti ndilibe Malamulo a Mulungu ai, popeza kuti ndili nawo malamulo a Khristu. Kwa amene ali ndi chikhulupiriro chofooka, ndidakhala ngati wa chikhulupiriro chofooka, kuti ndiŵakope ofookawo. Kwa anthu onse ndidakhala ngati iwo omwe, kuti ngati nkotheka ndikope ena mwa iwo. Zonsezi ndimazichita chifukwa cha Uthenga Wabwino, kuti inenso ndilandire nao madalitso a Uthengawo. Monga inu simudziŵa kuti pa mpikisano wa liŵiro onse amathamanga, koma mmodzi yekha ndiye amalandira mphotho? Tsono kuthamanga kwanu kukhale kwakuti nkukalandira mphothoyo. Aliyense wothamanga pa mpikisano wa liŵiro amadziletsa pa zonse. Iwowo amachita zimenezi kuti akalandire mphotho ya nkhata yamaluŵa yotha kufota. Koma mphotho imene ife tidzalandira, ndi yosafota. Nchifukwa chake ndimathamanga monga munthu wodziŵa kumene walinga. Ndiponso ndikamachita mpikisano womenyana, sindichita ngati munthu amene angomenya mophonya. Ndimazunza thupi langa ndi kuligonjetsa, kuti likhale ngati kapolo wondimvera. Ndimachita zimenezi kuwopa kuti ine ndemwe, amene ndidaitana ena ku mpikisano, ndingapezeke wosayenera kuchita nao mpikisanowo. Abale, ndifuna kuti mudziŵe zimene zidaŵachitikira makolo athu akale aja. Onse adayenda mu mthunzi wa mtambo, ndipo onse adaoloka Nyanja Yofiira. Motero mumtambomo ndi m'nyanjamo onsewo adachita ngati kubatizidwa ndi kukhala amodzi ndi Mose. Onse ankadya chakudya chauzimu chimodzimodzi. Onse ankamwanso chakumwa chauzimu chimodzimodzi, pakuti analikumwa m'thanthwe lauzimu limene linkaŵatsatira. Thanthwelo linali Khristu yemwe. Komabe ambirimbiri mwa iwo Mulungu sadakondwere nawo, kotero kuti adafera m'chipululu. Tsono zimene zidachitikazi ndi zitsanzo zotichenjeza ife, kuti tisamasirira zoipa monga adaachitira iwowo. Tisakhale opembedza mafano, monga analiri ena mwa iwo. Paja Malembo akuti, “Anthu adakhala pansi kuti adye ndi kumwa, kenaka nkuimirira kuti azivina.” Tisachite dama monga momwe adaachitira ena mwa iwo: paja pa tsiku limodzi adafa anthu zikwi makumi aŵiri ndi zitatu. Tisapute Ambuye monga momwe adaaŵaputira ena mwa iwo: paja anthuwo adaphedwa ndi njoka. Musadandaule monga momwe adaadandaulira ena mwa iwo: paja adaphedwa ndi mngelo wodzetsa imfa. Zonsezi zidaŵagwera makolo athuwo kuti zikhale zoŵachenjeza. Ndipo zidalembedwa kuti tipezepo phunziro ifeyo, amene tikuyandikira nthaŵi ya kutha kwa zonse. Tsono amene akuganiza kuti waimirira molimba, achenjere kuti angagwe. Mayeso amene inu mwakumana nawo, sasiyana ndi mayeso amene anthu ena onse adakumana nawo. Mulungu ndi wokhulupirika, sangalole kuti muyesedwe kopitirira mphamvu zanu. Koma pamene mudzayesedwa, Iye yemwe adzakukonzerani njira yopulumukira, pakukupatsani mphamvu kuti mupirire. Tsono okondedwa anga, pewani kupembedza mafano. Ndikulankhula nanu ngati anthu anzeru. Muweruze nokha zimene ndikunenazi. Nanga chikho chimene timachidalitsa mothokoza Mulungu, kodi suja timaphatikizana ndi magazi a Khristu tikamweramo? Nanga mkate umene timaunyema, kodi suja timaphatikizana ndi thupi la Khristu tikaudya? Popeza kuti mkate ndi umodzi wokha, ife tonse, ngakhale tili ambiri, ndife thupi limodzi, chifukwa tonse timagaŵana mkate umodzi womwewo. Onani zimene amachita Ayuda. Nanga amene amadyako zoperekedwa nsembe, kodi suja amachita nao miyambo ya pa guwa lansembelo? Tsono tanthauzo la zimene ndikunenazi nchiyani? Kodi ndiye kuti nsembe yoperekedwa kwa fano nkanthu? Kapena kuti fanolo nkanthu? Iyai, koma kuti zimene anthu akunja amapereka nsembe, amapereka kwa Satana, osati kwa Mulungu. Sindifuna kuti inu muyanjane ndi Satana. Simungathe kumwera m'chikho cha Ambuye nkumweranso m'chikho cha Satana. Simungathe kudyera pa tebulo la Ambuye nkudyeranso pa tebulo la Satana. Kodi tichite kuŵaputa dala Ambuye? Kodi mphamvu zathu nkupambana zao? Zinthu zonse nzololedwa, koma si zonse zili ndi phindu. Zonse nzololedwa, koma si zonse zimathandiza. Munthu asamangodzifunira yekha zabwino, koma makamaka azifunira anzake zabwino. Mungathe kudya nyama iliyonse imene amagulitsa pa msika, osafunsa mafunso okhudzana ndi m'mene mtima wanu umamvera. Paja Malembo akuti, “Dziko lapansi ndi zonse zam'menemo ndi za Chauta.” Mkunja akakuitanani kuti mukadye naye, inuyo nkuvomera kupitako, mukadye chilichonse chimene akakupatseni. Musakafunse mafunso okhudzana ndi m'mene mtima wanu umamvera. Koma wina akakuuzani kuti, “Nyama iyi idaperekedwa kwa mafano,” apo ndiye musadye nyamayo. Chifukwa cha amene wakuuzayo, usadye nyamayo, kuwopa kuti mtima ungavutike. Osati kuti iweyo ungavutike mu mtima ai, koma iye uja amene wakuuzayo. Pamenepo udzati, “Kodi ufulu wanga utsekerezedwe chifukwa munthu wina mtima wake ukumuvuta? Ngati ine ndikuthokoza Mulungu chifukwa cha chakudya changa, nanga munthu angandinyoze bwanji chifukwa cha chakudya chimene ndikuchilandira mothokoza Mulungu?” Tsono, kaya mulikudya, kaya mulikumwa, kaya mukuchita chilichonse, muzichita zonse kuti mulemekeze Mulungu. Moyo wanu ukhale wosaphunthwitsa Ayuda, kapena anthu a mitundu ina, kapenanso Mpingo wa Mulungu. Muzichita monga momwe ndimachitira ine. Ndimayesa kukondweretsa anthu onse pa zonse. Sindifunafuna zokomera ineyo, koma ndimafunafuna zokomera anthu onse, kuti apulumuke. Muzinditsanzira ine monga momwe inenso ndimatsanzira Khristu. Ndikukuyamikani chifukwa mumandikumbukira pa zonse, ndipo mumasunga miyambo imene ndidakusiyirani. Koma ndifuna kuti mudziŵe kuti Khristu ndiye mutu wa mwamuna aliyense, mwamuna ndiye mutu wa mkazi, ndipo Mulungu ndiye mutu wa Khristu. Ngati mwamuna apemphera kapena kulalika mau a Mulungu, atavala kanthu kumutu, akunyoza mutu wake. Koma mkazi akamapemphera kapena kulalika mau a Mulungu, osavala kanthu kumutu, akunyoza mutu wake. Kuteroko sikusiyana ndi kungometa mpala. Ngati mkazi sazivala kanthu kumutu, kunali bwino atangodula tsitsi lake. Koma popeza kuti nchamanyazi kwa mkazi kumeta mpala, kapena kudula tsitsi lake, ndiyetu azivala kanthu kumutu. Kwa mwamuna palibe chifukwa choti azivalira kanthu kumutu, pakuti amaonetsa maonekedwe ndi ulemerero wa Mulungu. Koma mkazi amaonetsa ulemerero wa mwamuna. Pajatu mwamuna sadapangidwe kuchokera kwa mkazi, koma mkazi ndiye adapangidwa kuchokera kwa mwamuna. Ndiponso mwamuna sadalengedwe chifukwa cha mkazi, koma mkazi ndiye adalengedwa chifukwa cha mwamuna. Tsono, chifukwa cha angelo, mkazi azivala kanthu kumutu, kuti chikhale chizindikiro cha ulemu wake. Komabe m'maso mwa Ambuye mkazi sali kanthu popanda mwamuna, ndiponso mwamuna sali kanthu popanda mkazi. Inde mkazi adapangidwa kuchokera kwa mwamuna, komanso tsopano mwamuna amabadwa mwa mkazi. Ndipo zinthu zonse zimachokera kwa Mulungu. Weruzani nokha ngati nkoyenera kuti mkazi azipembedza Mulungu osavala kanthu kumutu. Kodi chibadwa chathu chomwe sichitiphunzitsa kuti nchamanyazi kwa mwamuna kukhala ndi tsitsi lalitali, koma kuti kwa mkazi nchaulemu? Mulungu adapatsa mkazi tsitsi lalitali loti aziphimbira mutu wake. Tsono ngati wina afuna kutsutsapo pa zimenezi, ndingoti ife ndiponso mipingo ya Mulungu tilibe mwambo wina ai ndi womwewu basi. Tsopano pali mfundo ina imene sindingakuyamikireni. Ndiye kuti misonkhano yanu imabweretsa zoipa osati zabwino ai. Choyamba, ndikumva kuti mukamasonkhana mu mpingo, mumapatulana. Ndipo ndikhulupirira kuti zimenezi kwinaku nzoona. Nkofunika ndithu kuti pakhale kusiyana maganizo pakati panu, kuti amene ali okhoza pakati panu adziŵike. Pamene musonkhana pamodzi, chimene mumadyatu si Mgonero wa Ambuye. Inu mumati mukamadya, aliyense angoyambapo kudya chakudya chakechake, kotero kuti wina amakhala ndi njala, m'menemo wina waledzera. Zokuwonerani zimenezi! Kodi mulibe nyumba zomakadyeramo ndi kumweramo? Kodi kapena mufuna kunyazitsa Mpingo wa Mulungu ndi kuŵachititsa manyazi amene alibe kanthu, eti? Ndikuuzeni chiyani tsono? Ndingakuyamikeni ngati? Iyai, pa zimenezi sindingakuyamikeni konse. Inetu zimene ndidalandira kwa Ambuye ndi zimene nanenso ndidazipereka kwa inu, zakuti usiku umene adaperekedwa uja, Ambuye Yesu adaatenga mkate. Ndipo atathokoza Mulungu, adaunyemanyema nati, “Ili ndi thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi kuti muzindikumbukira.” Momwemonso atatha kudya, Ambuye Yesu adatenga chikho nati, “Chikhochi ndi chipangano chatsopano chotsimikizika ndi magazi anga. Nthaŵi zonse mukamamwa chikho chimenechi, muzindikumbukira.” Pakuti nthaŵi zonse mukamadya mkate umenewu, ndi kumwa chikho chimenechi, mumalalika imfa ya Ambuye, mpaka adzabwerenso. Nchifukwa chake tsono, munthu akadya mkate umenewu, kapena kumwa chikho cha Ambuyechi mosayenera, apalamula mlandu wonyoza thupi la Ambuye ndiponso magazi ao. Koma munthu aziyamba wadziwona bwino asanadyeko mkate umenewu ndi kumwa chikho chimenechi. Pakuti amene adya mkate umenewu ndi kumwa chikho chimenechi, koma osalizindikira thupi la Ambuye, akudziitanira chilango pamene akudya ndi kumwa. Nchifukwa chake ambiri mwa inu akudwala, akufooka, ndipo ena amwalirapo kale. Tikadadziyang'ana bwino, sitikadalangidwa. Koma Ambuye amatilanga, kuti tiphunzirepo nzeru, kuwopa kuti tingaimbidwe mlandu pamodzi ndi anthu odalira zapansipano. Tsono abale anga, pamene musonkhana kuti mudye Mgonero wa Ambuye, muzidikirana. Ngati wina ali ndi njala, ayambe wadya kwao, kuti Mulungu angakulangeni chifukwa cha kusonkhana kwanu. Koma zina zimene sindidatchule, ndidzazilongosola ndikabwera. Abale, ndifuna kuti muzindikire bwino za mphatso za Mzimu Woyera. Mukudziŵa kuti pamene munali akunja, anthu ankakusokezani mwa njira izi ndi izi, kukukokerani ku mafano osalankhula. Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti munthu amene Mzimu wa Mulungu amamtsogolera, sanganene kuti, “Yesu atembereredwe.” Ndiponso, munthu amene Mzimu Woyera samtsogolera, sanganene kuti, “Yesu ndi Ambuye.” Tsonotu pali mphatso zamitundumitundu, koma wozipereka ndi Mzimu Woyera mmodzimodzi. Pali njira zosiyanasiyana zotumikira, koma Ambuye amene timaŵatumikira ndi amodzimodzi. Pali mphamvu zosiyanasiyana, koma Mulungu ndi mmodzimodzi amene amagwiritsa ntchito mphamvu zonsezo mwa munthu aliyense. Mzimu Woyera amapatsa munthu aliyense mphatso yakutiyakuti yoti aigwiritse ntchito yopindulitsa anthu onse. Mzimu Woyera amapatsa munthu wina mphatso ya kulankhula zanzeru, ndipo Mzimu Woyera yemweyo amapatsa wina mphatso ya kulankhula mau olangiza anthu. Mzimu Woyera yemweyo amapatsa wina mphatso ya kukhulupirira, ndipo Mzimu Woyera mmodzi yemweyo amapatsa wina mphatso ya kuchiritsa matenda. Amapatsa wina mphamvu zochitira zozizwitsa, wina mphatso ya kulalika mau a Mulungu, wina nzeru za kusiyanitsa pakati pa zinthu zochokera kwa Mzimu Woyera ndi zochokera kwina. Amapatsa wina mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziŵika, ndipo amapatsa wina mphatso ya kutanthauzira zilankhulozo. Amene amachititsa anthu zonsezi ndi Mzimu Woyera mmodzi yemweyo. Amagaŵira munthu aliyense monga momwe Iye afuna kumgaŵira. Khristu ali ngati thupi limodzi limene lili ndi ziwalo zambiri. Ngakhale ziwalozo nzambiri, komabe thupilo ndi limodzi lokha. Pajatu ngakhale ndife Ayuda kapena a mitundu ina, akapolo kapena mfulu, tidabatizidwa mwa Mzimu Woyera mmodzimodzi kuti tikhale thupi limodzi. Ndipo tonse tidalandira nao Mzimu Woyera mmodzi yemweyo. Thupitu si chiwalo chimodzi chokha ai, koma lili ndi ziwalo zambiri. Nanga phazi litanena kuti, “Poti sindine dzanja, ndiye kuti sindine chiwalo cha thupi”, kodi silikhala chiwalo cha thupi chifukwa cha chimenecho? Nanga khutu litanena kuti, “Poti sindine diso, ndiye kuti sindine chiwalo cha thupi”, kodi silikhala chiwalo cha thupi chifukwa cha chimenecho? Kodi thupi lonse likadakhala diso lokha, bwenzi munthu akumva bwanji? Kapena thupi lonse likadakhala khutu lokha, bwenzi munthu akununkhiza bwanji? Koma m'mene ziliri Mulungu adaika chiwalo chilichonse pamalo pake m'thupi, monga momwe adafunira. Ziwalo zonse zikadangokhala chiwalo chimodzi, sipakadakhala thupi konse. Komatu ziwalo nzambiri, ngakhale thupi ndi limodzi lokha. Motero diso silingauze dzanja kuti, “Ndilibe nawe ntchito.” Ndiponso mutu sungauze mapazi kuti, “Ndilibe nanu ntchito.” Kwenikwenitu ziwalo zimene zimaoneka ngati zofooka, ndizo zofunika kopambana. Ziwalo zimene timaziyesa zotsika, ndizo timazilemekeza kopambana. Ndipo ziwalo za thupi lathu zimene zili zochititsa manyazi, ndizo timaziveka kopambana. Koma zimene zili zooneka bwino, nkosafunikira kuti tiziveke motero. Mulungu polumikiza ziwalo za thupi, adazilumikiza mwa njira yoti adapereka ulemu woposa kwa ziwalo zimene zimausoŵadi ulemuwo. Adachita zimenezi kuti pasakhale kugaŵikana m'thupi, koma kuti ziwalo zonse zizisamalirana. Chiwalo chimodzi chikamamva kuŵaŵa, ziwalo zonse zimamvanso kuŵaŵa. Chiwalo chimodzi chikamalandira ulemu, ziwalo zonse zimakondwa nao. Tsono inuyo nonse pamodzi ndinu thupi la Khristu, ndipo aliyense mwa inu ndi chiwalo cha thupilo. Mulungu mu Mpingo wake adaika anthu aŵa: poyamba atumwi, kachiŵiri aneneri, kachitatu aphunzitsi. Adaikanso anthu amene ali ndi mphamvu za kuchita zozizwitsa, ena amene ali ndi mphamvu za kuchiritsa matenda, ena amene ali ndi mphatso ya kulongosola ntchito, ndiponso ena amene ali ndi mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziŵika. Kodi onse ndi atumwi? Kodi onse ndi aneneri? Kodi onse ndi aphunzitsi? Kodi onse ali ndi mphamvu za kuchita zozizwitsa? Kodi onse ali ndi mphatso ya kuchiritsa matenda? Kodi onse angathe kulankhula zilankhulo zosadziŵika? Kodi onse angathe kuzitanthauzira? Iyai, koma inu muike mtima wanu pa mphatso zopambana. Tsonotu ndikuwonetseni njira yopambana kwenikweni: Ngakhale nditamalankhula zilankhulo za anthu kapenanso za angelo, koma ngati ndilibe chikondi, ndili ngati chitsulo chongolira, kapena chinganga chosokosera. Ngakhale nditakhala ndi mphatso ya uneneri, ngakhale nditamadziŵa zobisika zonse, ndi kumamvetsa zinthu zonse, ngakhale nditakhala ndi chikhulupiriro chachikulu chakuti ndingathe kusuntha mapiri, koma ngati ndilibe chikondi, sindili kanthu konse. Ndipo ngakhale nditagaŵira amphaŵi chuma changa chonse, kapena kupereka thupi langa kuti anthu alitenthe, koma ngati ndilibe chikondi, ndiye kuti changa palibe. Chikondi ncholeza mtima ndiponso nchofatsa. Chikondi chilibe kaduka, ndipo sichidzitamanda kapena kudzikuza. Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa. Sichikondwerera zosalungama, koma chimakondwerera choona. Chikondi chimakhululukira zonse, chimakhulupirira nthaŵi zonse, sichitaya mtima, ndipo chimapirira onse. Chikondi nchosatha. Uneneri udzatha, kulankhula zilankhulo zosadziŵika kudzalekeka, ndipo nzeru za anthu zidzatha. Paja timangodziŵa zinthu mopereŵera, ndipo kulalika kwathunso nkopereŵera, koma changwiro chikadzaoneka, chopereŵeracho chidzatha. Pamene ine ndinali mwana, ndinkalankhula mwachibwana, ndinkaganiza mwachibwana ndipo zinthu ndinkazitengera chibwana. Koma nditakula, ndidazileka zachibwanazo. Tsopano timaona zinthu ngati m'galasi, zosaoneka bwino kwenikweni. Koma pa nthaŵiyo tidzaona chamaso ndithu. Tsopano ndimangodziŵa mopereŵera, koma pa nthaŵiyo ndidzamvetsa kotheratu, monga momwe Mulungu akundidziŵira ine kotheratu. Choncho pakali pano zilipo zinthu zitatuzi: chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi. Koma mwa zonsezi chopambana ndi chikondi. Muziyesetsa kukhala nacho chikondi, komanso muike mtima pa mphatso zimene Mzimu Woyera amapereka, makamaka mphatso ya kulankhula mau ochokera kwa Mulungu. Munthutu wolankhula chilankhulo chosadziŵika, salankhula ndi anthu ai, koma ndi Mulungu. Palibe munthu womvetsa zimene iyeyo akunena, Mzimu Woyera ndiye amamlankhulitsa zachinsinsi. Koma wolankhula mau ochokera kwa Mulungu, amalankhula ndi anthu, ndipo amaŵathandiza, amaŵalimbitsa mtima ndi kuŵasangalatsa. Munthu wolankhula chilankhulo chosadziŵika, amangothandizidwa yekha, koma wolankhula mau ochokera kwa Mulungu, amathandiza mpingo. Ndikadakonda kuti nonsenu mukhale nayo mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziŵika, koma makamaka ndikadakonda kuti nonsenu mukhale ndi mphatso ya kulankhula mau ochokera kwa Mulungu. Pakuti munthu wolankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndiye wofunika kwambiri kuposa wolankhula zilankhulo zosadziŵika, ngati palibe munthu wotanthauzira zilankhulo, kuti mpingo upindulepo. Abale, mudzapindulanji ngati ndibwera kwa inu nkumadzalankhula m'zilankhulo zosadziŵika? Simudzapindula konse ndi kulankhula kwangako, ngati m'mau angawo mulibe zina zimene Mulungu wandiwululira, kapena zina zopatsa nzeru, kapena zina zimene Mulungu andipatsa kuti ndinene, kapenanso phunziro lina. Ndi ngati zipangizo zopanda moyo zimene zili ndi liwu, monga toliro kapena zeze. Woziliza akapanda kusiyanitsa bwino maliwu ake, womvera sangadziŵe nyimbo imene ikuimbidwa. Ndiponso woliza lipenga akapanda kuliliza momveka bwino, ndani angakonzekere nkhondo? Inunso chimodzimodzi: munthu angadziŵe bwanji zimene mukulankhula, ngati polankhula simunena mau omveka bwino? Pamenepo mudzangotaya mau anu pachabe. Mosapeneka konse pali zilankhulo zamitundumitundu pa dziko lapansi, ndipo palibe ndi chimodzi chomwe chimene mau ake alibe tanthauzo. Koma ngati ine sindidziŵa tanthauzo la mau a m'chilankhulo, ndidzakhala mlendo kwa amene akulankhula, ndipo iyenso adzakhala mlendo kwa ine. Inunso chimodzimodzi: popeza kuti mwaika mtima pa mphatso za Mzimu Woyera, muziyesetsa kuzigwiritsa ntchito, makamaka mphatso zolimbikitsa mpingo. Nchifukwa chake munthu wolankhula chilankhulo chosadziŵika, apemphere kuti alandirenso mphatso ya kuchitanthauzira. Ngati ndipemphera m'chilankhulo chosadziŵika, mtima wanga ukupemphera inde, koma nzeru zanga sizipindulapo kanthu pamenepo. Nanga pamenepa nkutani? Ndidzapemphera ndi mtima wanga, komanso ndi nzeru zanga. Ndidzaimba ndi mtima wanga, komanso ndi nzeru zanga. Mukayamika Mulungu ndi mtima wanu wokha, nanga munthu amene ali nanu pamodzi, koma sadziŵa zamumtimazo, angavomereze bwanji kuti, “Amen!” pa pemphero lanu lothokoza Mulungu, pamene sakudziŵa zimene inuyo mukunena. Ngakhale inu muthokoze Mulungu bwinobwino, koma munthu winayo sapindulapo konse. Ndikuthokoza Mulungu kuti ine ndimalankhula m'zilankhulo zosadziŵika kuposa nonsenu. Komabe mu msonkhano wa mpingo, m'malo molankhula mau ochuluka m'chilankhulo chosadziŵika, ndingakonde kwambiri kunena mau asanu okha omveka bwino, kuti ndiphunzitsire anthu. Abale, musamaganiza zachibwana. Pa zoipa, khalani ngati ana osadziŵa, koma pa maganizo anu, mukhale okhwima. M'Malembo mudalembedwa kuti, “Ndidzalankhula ndi mtundu uwu kudzera mwa anthu a zilankhulo zachilendo, ndiponso ndi pakamwa pa anthu achilendo. Koma ngakhale nditero, sadzandimvera, akutero Chauta.” Motero kulankhula m'zilankhulo zosadziŵika, ndi chizindikiro kwa anthu osakhulupirira, osati kwa anthu okhulupirira. Koma kulankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndi chizindikiro kwa anthu okhulupirira, osati kwa osakhulupirira. Tsono ngati mpingo wonse usonkhana pamodzi, ndipo onse ayamba kulankhula zilankhulo zosadziŵika, nanga mukaloŵa anthu osadziŵa kapena osakhulupirira, kodi iwo sadzayesa kuti ndinu amisala? Koma ngati onse alankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndipo munthu wosakhulupirira kapena wosadziŵa aloŵa, adzatsutsidwa ndi zonse zimene akumva. Mau onsewo adzamuloŵa mu mtima, ndipo zobisika za mumtima mwake zidzaonekera poyera. Pamenepo iye adzadzigwetsa choŵerama pansi ndi kupembedza Mulungu, ndipo adzavomereza kuti Mulungu ali pakati panudi. Ndiye titani tsono, abale? Pamene musonkhana pamodzi, aliyense angathe kukhala ndi nyimbo, kapena phunziro loti aphunzitse, kapena kanthu kena kamene Mulungu wamuululira, kapena mau oti alankhule m'chilankhulo chosadziŵika, ndipo wina afuna kutanthauzira mauwo. Komatu cholinga cha zonsezi chikhale kulimbikitsa mpingo. Ngati alipo ena ofuna kulankhula m'chilankhulo chosadziŵika, alankhule aŵiri okha, kapena atatu, koma osapitirira pamenepo. Alankhule modikirana, ndipo pakhale wina wotanthauzira mauwo. Koma ngati palibe munthu wotha kutanthauzira mauwo, iyeyo akhale chete mu msonkhano, ndipo azingolankhula ndi Mulungu payekha. Kunena za olankhula mau ochokera kwa Mulungu, aŵiri kapena atatu alankhule, ndipo ena onse aweruze zimene iwowo akunena. Koma Mulungu akaulula kanthu kwa munthu wina amene ali pomwepo, amene akulankhulayo akhale chete. Nonsenu mungathe kulankhula mau ochokera kwa Mulungu malinga nkupatsana mpata, kuti onse aphunzire ndi kulimbikitsidwa. Anthu amene ali ndi mphatso ya kulankhula mau ochokera kwa Mulungu, adziŵe kuilamulira mphatsoyo. Mulungu safuna chisokonezo ai, koma mtendere. Monga zimachitikira m'mipingo yonse ya anthu a Mulungu, akazi akhale chete m'misonkhano ya mpingo, pakuti iwo saloledwa kulankhula. Monga Malamulo a Mose anenera, akazi azikhala omvera. Ngati ali ndi mafunso, akafunse amuna ao kunyumba. Pajatu nchamanyazi kuti mkazi alankhule mu msonkhano wa mpingo. Monga nkuti mau a Mulungu adachokera kwa inu? Kaya kapena adafika kwa inu nokha? Ngati wina akuyesa kuti akulankhula mau ochokera kwa Mulungu, kapena kuti akuuzidwa mau ndi Mzimu Woyera, avomereze kuti zimene ndikukulemberanizi ndi lamulo lochokera kwa Ambuye. Ngati munthuyo savomereza zimenezi, Mulungunso samuvomereza iyeyo. Nchifukwa chake tsono, abale anga, ikani mtima pa kulankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndipo musaletse anthu kulankhula zilankhulo zosadziŵika. Koma tsono, zonse zizichitika moyenera ndi molongosoka. Abale, ndifuna kukukumbutsani Uthenga Wabwino umene ndidakulalikirani. Mudaulandira, ndipo mudakhazikitsapo chikhulupiriro chanu molimba. Mulungu adzakupulumutsani ndi Uthenga Wabwinowu, ngati musunga bwino mau ake monga ndidakulalikirani. Popanda kutero, bwenzi mutangokhulupirira pachabe. Pajatu mau aakulu amene ndidakupatsani ndi omwewo amene inenso ndidalandira. Mauwo ndi akuti Khristu adafera machimo athu, monga Malembo anenera. Adaikidwa m'manda, mkucha wake adauka, monga Malembo anenera. Motero adaonekera Kefa, kenaka atumwi khumi ndi aŵiri aja. Pambuyo pake adaonekera abale opitirira mazana asanu pa nthaŵi imodzi. Ambiri mwa iwowo akalipo, ena adamwalira. Ndipo adaonekera Yakobe, kenaka atumwi onse. Potsiriza, pambuyo pa onse adandiwonekeranso ineyo, ngakhale ndili ngati mpolo chabe. Inetu ndine wamng'onong'onodi mwa atumwi onse. Sindine woyenera konse kuti ndizitchedwa mtumwi, pakuti ndinkazunza Mpingo wa Mulungu. Koma chifukwa chakuti Mulungu adandikomera mtima, ndili monga ndilirimu. Ndipo kukoma mtima kwakeko sikunali kopanda phindu, popeza kuti ndidagwira ntchito koposa atumwi ena onse. Komabe si ndine ndidaigwira, koma mphamvu za Mulungu zimene zikundilimbikitsa. Motero kaya ndi ineyo kaya ndi iwowo, zimene timalalika ndi zomwezo, zimene mudakhulupirira ndi zomwezonso. Tsono popeza kuti chimene timalalika ndi chakuti Khristu adauka kwa akufa, bwanji ena mwa inu akunena kuti, “Anthu akufa sadzaukanso?” Ngati akufa sadzauka, ndiye kuti Khristunso sadauke. Tsono ngati Khristu sadauke, kulalika kwathu nkwachabe, ndipo chikhulupiriro chanu nchachabenso. Ngati zili choncho, ndiye kuti ndife mboni zonama, tikuchita umboni wonama m'dzina la Mulungu, ponena kuti Mulungu adaukitsa Khristu. Ngati nzoonadi kuti akufa sauka, ndiye kuti Mulungu sadamuukitse Khristuyo. Pakuti ngati akufa sauka, Khristunso sadauke. Ndipotu ngati Khristu sadauke, chikhulupiriro chanu nchopanda pake, ndipo mukadali m'machimo anu. Pamenepo nawonso amene adamwalira ali okhulupirira Khristu, adatayika ndithu. Ngati taika chikhulupiriro chathu mwa Khristu chifukwa cha moyo uno wokha, ndiye kuti ndife omvetsa chisoni koposa anthu ena onse. Koma ai, Khristu adauka ndithu kwa akufa. Pakati pa onse amene adafa, ndiye woyamba kuuka. Pakuti monga imfa idadza pansi pano kudzera mwa munthu wina, momwemonso kuuka kwa akufa kudadza kudzera mwa munthu wina. Monga anthu onse amamwalira chifukwa ndi ana a Adamu, momwemonso anthu onse adzauka chifukwa cholumikizana ndi Khristu. Koma aliyense adzauka pa nthaŵi yake: woyambirira ndi Khristu, ndipo pambuyo pake, pamene Khristuyo adzabwera, nawonso amene ali ake adzauka. Pamenepo chimalizo chidzafika. Khristu atathetsa ufumu wonse, ulamuliro wonse, ndi mphamvu zonse, adzapereka ufumu uja kwa Mulungu Atate. Paja Khristu ayenera kulamulira mpaka atagonjetsa adani ake onse. Mdani wotsiriza kumthetsa mphamvu, ndiye imfa. Malembotu akuti, “Mulungu adamgonjetsera zinthu zonse.” Koma nchodziŵikiratu kuti pamene akuti “zinthu zonse,” sakuphatikizapo ndi Mulungu yemwe, amene adagonjetsera Khristu zinthu zonse. Koma pamene zonse zidzakhala zitagonjera Khristu, pamenepo Mwana wa Mulungu nayenso adzagonjera Mulungu, amene adamgonjetsera zinthu zonse. Adzachita zimenezi kuti Mulungu akhale wolamulira aliyense kwathunthu. Ngati Yesu sadauke kwa akufa, nanga amafunanji anthu amene amabatizidwa m'malo mwa amene adafa? Ngati akufa sauka konse, nanga chifukwa chiyani anthu amabatizidwa m'malo mwao? Nanga pamenepo ifenso timakhaliranji m'zoopsa nthaŵi zonse? Abale anga, imfa ndimayenda nayo tsiku ndi tsiku. Ndikunenetsa zimenezi chifukwa ndimakunyadirani mwa Khristu Yesu Ambuye athu. Nanga pamene ndidalimbana ndi zilombo ku Efeso, ndidapindulapo chiyani, ngati ndinkatsata maganizo a anthu chabe? Ndiyetu ngati akufa sauka, tizingochita monga amanenera kuti, “Tiyeni tizidya ndi kumwa, pakuti maŵa tikufa.” Musadzinyenge. “Paja kuyanjana ndi anthu ochimwa kumaononga khalidwe.” Mudzidzimuke mumtima mwanu, ndipo muleke kuchimwa. Ena mwa inu sadziŵa Mulungu konse. Ndikukuuzani zimenezi kuti muchite manyazi. Koma kapena wina nkufunsa kuti, “Kodi akufa adzauka bwanji? Kodi adzakhala ndi thupi lotani?” Ati kupusa ati! Mbeu imene umafesa, siingamere ndi kukhala moyo itapanda kufa. Ndipo chimene ufesa, si mmera umene udzatuluka ai, koma ndi njere chabe, kaya ndi ya tirigu, kapena ya mtundu wina uliwonse. Koma Mulungu amaisandutsa mmera monga momwe Iye akufunira, mbeu iliyonse mmera wakutiwakuti. Mnofu sukhala wa mtundu umodzi. Pali mnofu wina wa anthu, wina wa nyama, wina wa mbalame, ndi wina wa nsomba. Palinso zolengedwa zakuthambo, ndi zina zapansipano. Koma ulemerero wa zakuthambo ndi wosiyana ndi ulemerero wa zapansipano. Dzuŵa lili ndi kuŵala kwake, mwezi uli ndi kuŵala kwake kosiyana ndi kwa dzuŵa kuja, nyenyezinso zili ndi kuŵala kwake kosiyana ndi kwa zina zija. Ngakhale nyenyezizo zimasiyananso kuŵala kwake. Zidzateronso pamene akufa adzauka. Thupi loikidwa m'nthaka ngati mbeu yofesa, limaola, koma likadzauka, lidzakhala losaola. Thupi loikidwa m'manda, ndi lonyozeka ndi lofooka, koma likadzauka lidzakhala lokongola ndi lamphamvu. Thupi loikidwa m'manda, ndi lamnofu chabe, koma likadzauka, lidzakhala lauzimu. Ngati pali thupi lamnofu, palinso thupi lauzimu. Paja Malembo akuti, “Munthu woyamba uja, Adamu, adachita kusanduka chinthu chamnofu chokhala ndi moyo.” Koma Adamu wotsiriza adakhala chinthu chauzimu chopatsa moyo. Loyamba si thupi lauzimu ai. Loyamba ndi lamnofu, pambuyo pake lauzimu. Adamu woyamba uja anali wochokera ku dothi, anali wapansipano. Koma Khristu, Adamu wachiŵiri uja, anali wochokera Kumwamba. Anthu onse apansipano ali ngati Adamu wopangidwa ndi dothi uja. Ndipo onse amene ali a Kumwamba, ali ngati Khristu wa Kumwamba. Monga takhala ofanafana ndi Adamu, munthu wopangidwa ndi dothi uja, momwemonso tidzakhala ofanafana ndi Khristu, munthu wa Kumwamba. Abale, chimene ndikunena nchakuti munthu ndi thupi lake lamnofuli sangathe kuloŵa mu Ufumu wa Mulungu, ndipo zimene zimaola, sizingathe kuloŵa kumene zinthu siziwola. Mvetsetsani, ndikuuzeni chinsinsi. Sikuti tonse tidzamwalira, komabe tonse tidzasandulika. Zidzachitika mwadzidzidzi, pa kamphindi ngati kuphethira kwa diso, pamene lipenga lotsiriza lidzalira. Likadzaliratu lipengalo, akufa adzauka ndi matupi amene sangaole, ndipo ife tidzasandulika. Pakuti thupi lotha kuwolali liyenera kusanduka losatha kuwola, ndipo thupi lotha kufali liyenera kusanduka losatha kufa. Tsono thupi lotha kuwolali likadzasanduka losatha kuwola, ndipo thupi lotha kufali likadzasanduka losatha kufa, pamenepo zidzachitikadi zimene Malembo adanena kuti, “Imfa yagonjetsedwa kwathunthu.” “Iwe imfa, kupambana kwako kuli kuti? Iwe imfa, ululu wako uli kuti?” Ululu wake wa imfa ndi uchimo, ndipo chimene chimapatsa uchimo mphamvu, ndi Malamulo. Koma tiyamike Mulungu amene amatipambanitsa mwa Ambuye athu Yesu Khristu. Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu. Kunena za zopereka zothandizira akhristu a ku Yerusalemu, inunso muchite monga momwe ndidalongosolera m'mipingo ya ku Galatiya. Pa tsiku loyamba la sabata, aliyense mwa inu azipatulapo kanthu, potsata momwe wapezera. Zimene wapatulazo azisunge kunyumba, kuti pasakakhalenso kusonkhasonkha ine ndikabwera. Tsono ndikadzafika, ndidzaŵapatsa makalata anthu amene mungaŵasankhe, ndipo ndidzaŵatuma kuti akapereke mphatso yanuyo ku Yerusalemu. Koma ngati nkofunika kuti inenso ndipite, tidzapitira limodzi. Ndidzafika kwanuko nditadutsa dziko la Masedoniya, pakuti ndingodzerako ku Masedoniyako. Koma kapena kwanuko ndidzakhala kanthaŵi, kapenanso nyengo yonse yachisanu. Ndifuna kuti pambuyo pake mudzandithandize kupitiriza ulendo wanga kulikonse kumene ndingapite. Ulendo umenewo sindifuna kungokuwonani chidule modutsa chabe, koma ndikuyembekeza kukhala nanu kanthaŵi ndithu, Ambuye akalola. Koma ndikhala ku Efeso kuno mpaka chikondwerero cha Pentekoste. Pakuti pano mwai ulipo woti nkuchita zazikulu, ndiponsotu adani alipo ambiri. Ngati Timoteo afika kwanuko, samalani kuti pasakhale kanthu komdetsa nkhaŵa pakati panu, pakuti iyenso akugwira ntchito ya Ambuye, monga ine. Tsono wina aliyense asamnyoze, koma mumthandize kupitiriza ulendo wake mwamtendere kubwerera kuli ine kuno. Paja ndikumuyembekeza pamodzi ndi abale ena. Kunena za mbale wathu, Apolo, ndamuumiriza kolimba kuti pamodzi ndi abale ena abwere kwanuko kudzakuwonani, koma iye sadafune kupita tsopano. Akadzapeza mpata wabwino, adzabwera. Khalani maso, khalani okhazikika m'chikhulupiriro chanu, chitani chamuna, khalani amphamvu. Zonse zimene muchita, muzichite mwachikondi. Abale, mukudziŵa kuti Stefanasi ndi a m'banja mwake ndiwo adayambirira kuloŵa chikhristu m'dziko la Akaiya. Ndipo akhala akudzipereka kutumikira anthu a Mulungu. Tsono ndikukupemphani kuti inunso muziŵamvera anthu otere, ndiponso aliyense wogwira ntchito ndi kutumikira modzipereka pamodzi nawo. Ndakondwa kuti Stefanasi, Fortunato ndi Akaiko afika, pakuti ngakhale inu simuli nane, iwo achita ngati kuloŵa m'malo wanu. Adandisangulutsa ine monga adasangulutsanso inu. Anthu otere muziŵalemekeza. Mipingo ya ku dziko la Asiya ikuti moni. Akwila ndi Prisika, pamodzi ndi mpingo umene umasonkhana m'nyumba mwao, akuti moni kwa inu nonse, akhristu anzao. Abale onse akuti moni. Mupatsane moni mwa chikondi chenicheni. Ineyo Paulo, ndikuchita kulemba ndekha mau aŵa akuti “Moni.” Ngati munthu sakonda Ambuye, akhale wotembereredwa. Maranatha! Ambuye athu, bwerani! Ambuye Yesu akudalitseni. Chikondi changa chikhale pa inu nonse, mwa Khristu Yesu. Ndine, Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa kufuna kwa Mulungu. Ndili limodzi ndi mbale wathu Timoteo. Tikulembera mpingo wa Mulungu umene uli ku Korinto, ndiponso anthu onse a Mulungu okhala m'dziko lonse la Akaiya. Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere. Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Ndiwo Atate a chifundo ndi otilimbitsa mtima kwathunthu. Mulungu amatilimbitsa mtima m'masautso athu onse, kuti monga momwe Iye amalimbitsira ife mtima, nafenso tithe kuŵalimbitsa mtima anzathu amene ali pakati pa masautso amitundumitundu. Pakuti monga tikumva zoŵaŵa kwambiri pamodzi ndi Khristu, momwemonso Khristu amatilimbitsa mtima kwambiri. Ngati tikuzunzika, nkuti inu mupeze chokulimbitsani mtima ndiponso chipulumutso. Ngati ife atilimbitsa mtima, nkuti inunso mulimbitsidwe mtima ndi kulandira mphamvu za kupirira pamene mulikumva zoŵaŵa zomwezo zimene ifenso timamva. Chikhulupiriro chathu pa inu ncholimba. Tikudziŵa kuti monga mulikumva zoŵaŵa pamodzi nafe, momwemonso mudzapeza chokulimbitsani mtima pamodzi nafe. Tsono abale, tifuna kuti mudziŵe, masautso amene tidakumana nawo ku dziko la Asiya, adatipsinja koopsa, kopitirira mphamvu zathu, kotero kuti sitinkayembekezanso kuti nkukhala ndi moyo. Ndithu m'mitima mwathu tinkangoganiza kuti basi talandira chilango chokaphedwa. Zimenezi zidachitika kuti tisamadzikhulupirire, koma kuti tizikhulupirira Mulungu amene amaukitsa akufa. Ndiye amene adatipulumutsa ku zoopsa zotere za imfa, ndipo adzatipulumutsanso. Taika ndithu chikhulupiriro chathu pa Iyeyo choti adzatipulumutsanso. Inu nomwe muthandizane nafe pakutipempherera. Pamenepo anthu ambiri adzathokoza Mulungu m'malo mwathu, chifukwa cha zimene Iye adatichitira mwa kukoma mtima kwake. Chimene timanyadira nchakuti mtima wathu umatichitira umboni kuti ponseponse pamene tidapita, koma makamakanso pakati panu, mayendedwe athu anali oyera ndi opanda chinyengo. Zinali choncho osati chifukwa chotsata nzeru za anthu ai, koma chifukwa Mulungu adatikomera mtima. Timakulemberani zokhazokha zimene mungathe kuziŵerenga ndi kuzimvetsa bwino. Ndikhulupirira kuti, monga mwayamba kale kutidziŵa pang'ono, mudzatidziŵa kwenikweni, ndiye kuti pa tsiku la Ambuye Yesu mudzatha kutinyadira ife, monga momwe ifenso tidzakunyadirani inu. Popeza kuti pa zimenezi ndinali wotsimikiza ndithu, ndidaaganiza zoti ndiyambe ndafika kwanuko. Ndidaafuna kuti mulandire madalitso paŵiri: ndidaakonza ulendo wanga kuti ndidzere kwanu popita ku Masedoniya, ndi kuti ndidzerenso kwanu pochokera ku Masedoniyako. Ndinkafuna kuti potero mudzandithandize kupitiriza ulendo wanga wopita ku Yudeya. Kodi pamene ndidaaganiza kuchita zimenezi, inu mukuyesa kuti ndidaachita zinthu mwachibwana? Kaya zimene ndimaganiza kuzichita, kodi ndimangoziganiza mwaukapsala, kotero kuti ndingathe kunena kuti, “Inde, inde” ndiponso “Ai, ai” pa nthaŵi imodzi? Pali Mulungu woona, ndikulumbira kuti mau athu amene timakuuzani sali “Inde” ndiponso “Ai”. Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, amene ine ndi Silivano ndi Timoteo tidakulalikirani, sanali “Inde” ndiponso “Ai” pa nthaŵi imodzi, koma nthaŵi zonse anali “Inde” wa Mulungu. Ndipo zonse zimene Mulungu adalonjeza zidachitika ndi “Inde” ameneyu. Nchifukwa chake mwa Yesu Khristuyo timanena kuti, “Amen” kulemekeza Mulungu. Mulungu ndi amene amatikhazikitsa pamodzi nanu mwa Khristu. Ndiye amene adatidzoza, natisindikiza chizindikiro chake, ndi kuika Mzimu Woyera m'mitima mwathu ngati chikole. Mulungu akhale mboni yanga, chifukwa chenicheni chimene sindidafikirenso ku Korinto chinali chakuti ndisakumvetseni chisoni. Sikuti tikufuna kuchita ngati kukulamulirani pa zoti muzikhulupirira, pakuti pa mbali ya chikhulupiriro chanu, ndinu okhazikika ndithu. Makamaka tingofuna kugwirizana nanu kuti mukhale okondwa. Nchifukwa chake ndidatsimikiza kuti ndisachite ulendo winanso wopweteka wobwera kwanuko. Ngati ndine amene ndikukupweteketsani mtima, nanga ineyo adzandisangalatsa ndani, kodi si yemweyo amene ndidampweteketsa mtima. Nchifukwa chake ndidakulemberani kalata ija. Sindidafune kudza kwanuko, kuwopa kuti inuyo oyenera kundisangalatsanu mungandipweteketse mtima. Ndidaadziŵiratu kuti ine ndikamakondwa, nonsenunso mumakondwa. Pamene ndidakulemberani kalata ija, mtima wanga unali wovutika ndi wopsinjika ndithu, ndipo ndinkalira misozi. Sindidafune kukupweteketsani mtima, koma makamaka ndinkafuna kuti mudziŵe kuti ndimakukondani kwambiri. Ngati wina aliyense adachita kanthu kolasa mtima, si ineyo amene adalasa mtima, koma pang'ono ponse adalasako nonsenu, kunenatu mosakulitsa nkhani. Munthu woteroyo, pafupi nonse mwamtsutsa, choncho chilangocho nchokwanira. Tsono makamaka nkwabwino mumkhululukire ndi kumlimbitsa mtima, kuwopa kuti angamve chisoni chachikulu chomtayitsa mtima kotheratu. Nchifukwa chake ndikukupemphani kuti mumtsimikizirenso kuti mumamkonda ndithu. Pamene ndinkakulemberani kalata ija, cholinga changa chinali chakuti ndikuyeseni, ndi kuwona ngati mudzandimvera pa zonse. Mukakhululukira munthu, inenso ndimkhululukira. Ngati ine ndakhululukira, patakhala kanthu koti ndakhululukira, ndiye kuti ndakhululukira chifukwa cha inu pamaso pa Khristu. Cholinga chake nkuti Satana asatichenjerere, paja tikudziŵa njira zake. Pamene ndidafika ku Troasi kuti ndikalalike Uthenga Wabwino wonena za Khristu, ndidapeza Ambuye atanditsekulira kale pa khomo kuti ndikagwire ntchito kumeneko. Komabe mumtima mwanga munalibe mtendere, chifukwa sindidampeze Tito, mbale wanga. Tsono ndidatsazikana ndi anthu akumeneko nkupita ku Masedoniya. Tithokoze Mulungu amene mwa Khristu amatitsogolera nthaŵi zonse m'kupambana kwake. Kudzera mwa ife Mulungu akupatsa anthu onse nzeru zodziŵira Khristu, ndipo nzeruzo zikuwanda ponseponse ngati fungo labwino. Zoonadi tili ngati fungo labwino la Khristu lokomera Mulungu, pakati pa anthu amene akupulumuka ndi amene akutayika. Kwa amene akutayika, fungoli ndi la imfa, ndipo limaŵapha. Koma kwa amene akupulumuka, fungoli ndi la moyo, ndipo limaŵapatsa moyo. Nanga ndani angaithe ntchito yotere? Ifetu sitili ngati anthu ena ambiri amene amangochita malonda ndi mau a Mulungu. Koma, popeza kuti tili mwa Khristu, ngati anthu otumidwa ndi Mulungu, timalankhula moona, molingana ndi kufuna kwake. Kodi ponena izi ndiye kuti tikuyamba kudzichitira umboni tokha? Kodi kapena nkofunika kuti ifenso, monga anthu ena, tikhale ndi makalata otichitira umboni kwa inu, kapena makalata aumboni ochokera kwa inu? Kalata yotichitira umboniyo ndinu nomwe. Idalembedwa m'mitima mwathu, kuti anthu onse aidziŵe ndi kumaiŵerenga. Anthu onse angathe kuwona kuti ndinu kalata yochokera kwa Khristu, yolembedwa kudzera mwa ife, osati ndi inki koma ndi mzimu wa Mulungu wamoyo, osati pa zolembapo zamiyala koma m'mitima mwa anthu. Mulungu akudziŵa kuti tikunena zimenezi chifukwa Khristu ndiye amatipatsa kulimba mtima kotere. Pakuti mwa ife tokha mulibe kanthu kamene kangatiganizitse kuti tingathe kuchita ntchitoyi patokha. Amene amatipatsa mphamvu ndi Mulungu kuti tithe kuichita. Ndiye amene adatipatsa mphamvu kuti tikhale otumikira chipangano chatsopano, osati mwa malamulo olembedwa, koma mwa Mzimu Woyera. Paja malamulo olembedwa amadzetsa imfa, koma Mzimu Woyera amapatsa moyo. Malamulo ongolembedwa pa miyala aja adaperekedwa ndi ulemerero waukulu, kotero kuti Aisraele sankatha kuyang'anitsitsa nkhope ya Mose chifukwa cha kuŵala kwake. Komabe kuŵala kwakeko kunali kosakhalitsa. Tsono ngati malamulowo, amene ali odzetsa imfa, adaperekedwa ndi ulemerero wotere, nanji ntchito ya Mzimu Woyera, kodi siidzakhala ndi ulemerero wopambana pamenepo? Ngati ntchito yoweruza anthu kuti alangidwe inali yaulemerero, ndiye kuti ntchito yoti anthu apezeke olungama pamaso pa Mulungu idzakhala yaulemerero koposa. Chifukwa cha ulemerero wopambanawu umene waoneka tsopano, zinthu zimene kale zidaali ndi ulemerero, masiku ano zilibenso ulemerero konse. Tsono ngati zinthu zosakhalitsa zidaafika ndi ulemerero, ndiye kuti zinthu zokhala mpaka muyaya zidzakhala ndi ulemerero wopambana. Popeza kuti timayembekeza zimenezi, timalimba mtima kwambiri. Sitichita ngati Mose amene ankaphimba nkhope yake ndi nsalu, kuwopa kuti Aisraele angamapenye kutha kwake kwa kuŵala kosakhalitsa kuja. Koma iwo nzeru zao zidauma, pakuti mpaka lero lino chophimba chomwe chija chimakhalapobe akamaŵerenga mabuku a m'Chipangano Chakale. Pajatu chophimbacho chimachotsedwa pokhapokha munthu akakhala mwa Khristu. Ndithu, mpaka lero lino nthaŵi zonse akamaŵerenga Malamulo a Mose, chophimba chija chimaphimbabe mitima yao. Koma munthu akatembenukira kwa Ambuye, chophimbacho chimachotsedwa. Tsono tikamati, “Ambuye,” tikunena Mzimu Woyera. Ndipo kumene kuli Mzimu wa Ambuye, kuli ufulu. Tonsefe, opanda chophimba nkhope yathu, timaonetsa ulemerero wa Ambuye, monga momwe galasi limaonetsera nkhope ya munthu. Monsemo Ambuye, amene ali Mzimu, amatisandutsa kuti tifanefane naye, ndi kukhala nawo ulemerero wake mochulukirachulukira. Mulungu mwa chifundo chake adatipatsa ntchitoyi, nchifukwa chake sititaya mtima. Takaniratu njira zonse zochititsa manyazi zimene anthu amatsata mobisika. Sitichita kanthu monyenga kapena kupotoza mau a Mulungu; koma pakulankhula zoona poyera pamaso pa Mulungu, tifuna kuti anthu onse ativomereze m'mitima mwao. Koma ngakhale Uthenga Wabwino umene timalalika uli wophimbika, ngwophimbika kwa okhawo amene akutayika. Iwoŵa sakhulupirira, popeza kuti Satana, amene ali mulungu wa dziko lino lapansi, adachititsa khungu maganizo ao, kuwopa kuti angaone kuŵala kwa Uthenga Wabwino. Kuŵalako kumaonetsa ulemerero wa Khristu, ndipo mwa Iyeyu Mulungu mwini amaoneka. Motero polalika sitidzilalika tokha, koma timalalika Yesu Khristu, kuti ndiye Ambuye. Ife ndife atumiki anu chabe chifukwa cha Yesuyo. Paja ndi Mulungu amene adaati, “Kuŵala kuunike kuchokera mu mdima.” Mulungu yemweyo ndiye adatiwunikiranso m'mitima mwathu, kuti anthu adziŵe ulemerero wa Mulungu umene ukuŵala pa nkhope ya Khristu. Koma ife ndife mbiya zadothi chabe zosungiramo chumachi, kuti padziŵike kuti mphamvu zazikulu zoterezi ndi za Mulungu, osati zathu ai. Tikuwona masautso a mtundu uliwonse, koma osapsinjidwa. Tikuthedwa nzeru, koma osataya mtima. Adani akutizunza, koma sitisoŵa wotithandiza. Akutigwetsa pansi, koma sitikugonja. Nthaŵi zonse tikuyenda nayo imfa ya Yesu m'thupi mwathu, kuti moyo wake uwonekenso m'thupi mwathu. Pakuti nthaŵi zonse, ngakhale tili ndi moyo, tikuperekedwa ku imfa chifukwa cha Yesu, kuti moyo wake uwonekenso m'matupi athu amene amafa. Motero ife timaperekedwa ku imfa, koma chimenechi chimakupatsani moyo. Malembo akuti, “Ndidakhulupirira, nchifukwa chake ndidalankhula.” Tsono popeza kuti ife tili ndi mtima womwewo wokhulupirira, ifenso timalankhula. Pakuti tikudziŵa kuti Mulungu amene adaukitsa Ambuye Yesu kwa akufa, adzatiwukitsa ifenso pamodzi ndi Yesu, nadzatifikitsa pamodzi nanu pamaso pake. Cholinga cha zonsezi nchakuti inu mupindule, ndipo kuti monga momwe anthu olandira madalitso a Mulungu akunka nachulukirachulukira, momwemonso othokoza Mulungu achulukirechulukire ndi kumchitira ulemu. Nchifukwa chake sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifookerafookera, komabe mu mtima tikulandira mphamvu yatsopano tsiku ndi tsiku. Masautso athu ndi opepuka, a nthaŵi yochepa, komabe akutitengera ulemerero umene uli waukulu kopambana, ndiponso wamuyaya. Mitima yathu siili pa zinthu zooneka, koma pa zinthu zosaoneka. Paja zooneka nzosakhalitsa, koma zosaoneka ndiye zamuyaya. Thupi limene timakhalamo pansi pano lili ngati msasa chabe. Koma tikudziŵa kuti msasawu ukadzapasuka, tidzakhala ndi nyumba ina imene Mulungu adatikonzera Kumwamba. Nyumbayo ndi yosamangidwa ndi manja a anthu, ndipo ndi yamuyaya. Nchifukwa chake tsono tikubuula ndi kulakalaka kuvala nyumba yathu yakumwambayo, kuti titaivala, tisadzapezeke amaliseche. Ife amene tili mu msasa uno timalemedwa ndipo timabuula. Sitifuna kuuvula msasawu ai, koma kwenikweni tikadakonda kuvala nyumba ija ya Kumwamba pamwamba pake, kuti chimene chili chakufa chimizidwe ndi moyo. Mulungu ndiye amene adatikonzeratu kuti tilandire zimenezi, ndipo adatipatsa Mzimu Woyera ngati chikole chake. Nchifukwa chake timalimba mtima masiku onse, ndipo tikudziŵa kuti nthaŵi yonse pamene tikukhala m'thupi, ngati kwathu, ndiye kuti tili kutali ndi Ambuye. Pakuti timatsata chikhulupiriro, osati zopenya ndi maso. Ndithu tikulimba mtima, ndipo makamaka tikadakonda kutuluka m'thupi lathu lino ndi kukakhala kwa Ambuye. Nchifukwa chake, ngakhale tikhalebe kuno, kapena tikakhale kwa Ambuye, timayesetsa kuŵakondweretsa Ambuyewo. Pakuti tonsefe tiyenera kukaimirira poyera pamaso pa Khristu kuti atiweruze. Kumeneko aliyense adzalandira zomuyenerera, molingana ndi zimene adachita pansi pano, zabwino kapena zoipa. Tsono popeza tikudziŵa kuti Ambuye ngoyenera kuŵaopa, timayesetsa kukopa anthu. Mulungu amatidziŵa kwathunthu, ndipo tikhulupirira kuti inunso mumatidziŵa kwenikweni m'mitima mwanu. Sitikuyesa kudzichitiranso umboni pamaso panu ai, koma tingofuna kukupatsani chifukwa choti muzitinyadira. Tikufuna kuti mukhale ndi kanthu koŵayankha amene angonyadira zooneka ndi maso, osati zamumtima. Ngati tidachita ngati tapenga, tidachita zimenezi kuti tilemekeze Mulungu. Koma ngati tikuchita zanzeru, tikuchita zanzeru kuti tikuthandizeni. Chikondi cha Khristu ndicho chimatiwongolera mokakamiza, popeza kuti tikudziŵa mosakayika konse kuti Munthu mmodzi adafera anthu onse, ndiye kuti pamenepo onse adafa. Iye adafera anthu onse, kuti amene ali ndi moyo, asakhalenso ndi moyo wofuna kungodzikondweretsa okha, koma azikondweretsa Iye amene adaŵafera, nauka kwa akufa chifukwa cha iwowo. Nchifukwa chake kuyambira tsopano ife sitiganiziranso za munthu aliyense potsata nzeru za anthu chabe. Ngakhale kale tinkaganiza za Khristu potsata nzeru za anthu chabe, koma tsopano sitiganizanso za Iye motero. Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano. Wochita zonsezi ndi Mulungu, amene mwa Khristu adatiyanjanitsa ndi Iye mwini, ndipo adatipatsa ntchito yolalikira anthu chiyanjanitsocho. Ndiye kuti mwa Khristu Mulungu ankayanjanitsa anthu a pa dziko lonse lapansi ndi Iye mwini, osaŵaŵerengera machimo ao. Ndipo adatipatsa ifeyo mau onena za chiyanjanitsocho kuti tiŵalalike. Tsono ndife akazembe oimirira Khristu, ndipo kudzera mwa ifeyo Mulungu mwini ndiye akulankhula nanu mokudandaulirani. Tikukupemphani m'dzina la Khristu kuti muvomere kuyanjananso ndi Mulungu. Khristu sadachimwe konse, koma Mulungu adamsandutsa uchimo chifukwa cha ife, kuti mwa Iyeyo ife tisanduke olungama pamaso pa Mulungu. Tsono popeza kuti ndife ogwirizana ndi Mulungu pa ntchito yake, takupembani musaŵasandutse achabe madalitso amene Mulungu adakupatsani. Paja Mulungu akuti, “Pa nthaŵi yanga yabwino ya kukomera anthu mtima, ndidakumvera, pa nyengo ya kupulumutsa anthu, ndidakuthandiza.” Mvetsani, ndi inotu nthaŵi yabwinoyo, imene Mulungu akukomera anthu mtima. Ndi Lerotu tsiku la chipulumutsolo. Sitifuna kupatsa anthu chifukwa chonyozera ntchito yathu, nchifukwa chake sitikhumudwitsa munthu aliyense ndi kanthu kalikonse. Koma pa zonse timasonyeza kuti ndife atumiki a Mulungu pakupirira kwambiri m'masautso, m'zoŵaŵa ndiponso m'nkhaŵa. Tidakwapulidwa, tidaponyedwa m'ndende, ndipo anthu adatiwukira mwachipolowe. Tidagwira ntchito kwambiri, mwina osagona tulo, osaona chakudya. Timatsimikiza kuti ndife atumiki a Mulungu pakuyera mtima, pakudziŵa zinthu mozama, pakuleza mtima, pakukoma mtima, mwa Mzimu Woyera, mwa chikondi chosanyenga, mwa mau oona, ndiponso mwa mphamvu ya Mulungu. Zida zimene zili m'dzanja lathu lamanja ndi lamanzere ndizo chilungamo. Anthu amatilemekeza, komanso amatinyoza. Amatinenera zoipa, komanso zabwino. Anthu amatiyesa onyenga, komabe ndife oona. Amatiyesa osadziŵika, komabe ndife odziŵika kwambiri. Amatiyesa anthu amene alikufa, komabe onani, tili moyo. Amatiyesa olangidwa, komabe sitidaphedwe. Amatiyesa achisoni, komabe ndife okondwa masiku onse. Amatiyesa amphaŵi, komabe timalemeretsa anthu ambiri. Amatiyesa opanda kanthu, komabe tili ndi zonse. Inu anthu a ku Korinto, talankhula nanu momasuka, ndipo tatsekula mtima wathu ndithu. Malo sakusoŵani mumtima mwathu, koma mumtima mwanu ndimo mukusoŵa malo. Ndikulankhula nanu ngati ana anga. Mutibwezere zomwezo zimene ifenso tidakuchitirani inu, pakutitsekulira mtima wanu. Musamagwirizana ndi anthu akunja, monga ngati kuti iwo ndi inu mumafanana. Nanga kulungama kungagwirizane bwanji ndi kusalungama? Kapena kuŵala kungayanjane bwanji ndi mdima? Kodi Khristu nkuvomerezana ndi Satana? Kodi mkhristu ndi mkunja angagaŵanenso chiyani pamodzi? Kodi Nyumba ya Mulungu nkufanana bwanji ndi mafano? Pajatu ife ndife Nyumba ya Mulungu wamoyo, monga Mulungu mwini adanena kuti, “Ndidzakhazikika mwa iwo, ndi kukhala nawo. Ndidzakhala Mulungu wao, iwo adzakhala anthu angaanga.” Nchifukwa chake Ambuye akuti, “Tulukani pakati pao, ndi kudzipatula. Musakhudze kanthu kosayera, ndipo ndidzakulandirani. Ndidzakhala Atate anu, inu mudzakhala ana anga aamuna ndi aakazi, akutero Ambuye Mphambe.” Tsono, inu okondedwa, popeza kuti tili ndi malonjezo ameneŵa, tiyeni tidzichotsere zinthu zonse zodetsa thupi lathu kapena mtima wathu. Ndipo pakuwopa Mulungu tiziyesetsa ndithu kukhala oyera mtima. Mutipatse malo m'mitima mwanu. Sitidalakwire munthu aliyense, kapena kumuipitsa, kapena kumchenjerera. Sindikunena zimenezi kuti mupezeke olakwa. Paja monga ndanena kale, inu muli m'mitima mwathu ndithu, kotero kuti tili pamodzi, ngakhale tikhale moyo kapena timwalire. Ndimakukhulupirirani kwambiri, ndipo ndimakunyadirani kwenikweni. Zondilimbitsa mtima zandichulukira, ndipo m'zovuta zathu zonse ndakondwa kopambana. Ngakhale pamene tidafika ku Masedoniya sitidapeze mpumulo konse. Tidapeza zovuta ponseponse, popeza kuti panali kukangana ndi adani otizungulira, ndiponso mantha m'mitima mwathu. Koma Mulungu amene amalimbitsa otaya mtima, adatilimbitsa ndi kufika kwa Tito. Ndipo chimene chidatilimbitsa, si kufika kwake kokha, koma makamakanso mau ake onena za m'mene iyeyo mudamlimbitsira mtima. Adatiwuza kuti mukulakalaka kundiwona, kuti muli ndi chisoni, ndiponso kuti mukuchita changu kundithandiza. Nchifukwa chake ndakondwa koposa. Kalata yanga ija idakupwetekani mtima, komabe sindikuchita chisoni kuti ndidailemba. Ndidaachita chisoni poyamba, ndipo ndikuwona kuti kalatayo idakupwetekanidi mtima, ngakhale kanthaŵi pang'ono chabe. Koma tsopano ndakondwa, osati chifukwa ndidaakupwetekani mtima, koma chifukwa kuvutika kwanu kudakuthandizani kutembenuka mtima. Kuvutika kwanuko kunali kovomerezeka ndi Mulungu, motero sitidakutayitseni kanthu kabwino kalikonse. Paja chisoni chokomera Mulungu chimamtembenuza munthu ndi kumpulumutsa, kotero kuti chisoni chake chimathera pomwepo. Koma kumva chisoni monga m'mene amachitira anthu odalira zapansipano, kumadzetsa imfa. Onani zimene chisoni chanu chokomera Mulungu chija chakuchitirani: chakupatsani changu chachikulu, chakukakamizani kwambiri kutsimikiza kuti simudalakwe, chakukwiyitsani kwambiri, ndipo chakuchititsani mantha aakulu. Chakulakalakitsani kuti mundiwone, ndipo chakupatsani changu chonditchinjiriza, ndiponso cholanga olakwa. Pa nkhani yonseyi umboni ulipo wakuti inu simudalakwepo. Motero, ngakhale ndidakulemberani kalata imene ija, sindidailembe chifukwa cha amene adalakwa uja, kapena chifukwa cha amene iyeyo adamlakwira. Koma ndidailemba kuti ndikuwonetseni pamaso pa Mulungu kuti changu chanu chotitchinjiriza nchachikulu ndithu. Zimenezi zatilimbitsa mtima kwambiri. Kuwonjezera pa zotilimbitsa mtimazo, chimwemwe cha Tito chidatikondweretsa kopambana, popeza kuti nonsenu mudamsangulutsa. Ndidamuuzadi kuti ndimakunyadirani, ndipo inu simudandichititse manyazi. Koma monga momwe zonse zimene tidaakuuzani zinali zoona, momwemonso kudaoneka kuti zimene ndidauza Tito mokunyadirani, zinali zoona. Makamaka chikondi chake pa inu nchachikulu kopambana pamene akumbukira kuti nonsenu mudamvera mau anga, ndipo mudamlandira ndi mantha ndi monjenjemerera. Ndikukondwa kuti ndingathe kukukhulupirirani pa zonse. Abale, tifuna kuti mudziŵe za m'mene Mulungu adadalitsira mipingo ya ku Masedoniya. Anthu a m'mipingoyo adayesedwa kwambiri ndi masautso, komabe adakondwa kwakukulu, kotero kuti adapereka moolowa manja kwenikweni, ngakhale anali amphaŵi. Ine ndikuŵachitira umboni kuti adapereka monga adathera, ngakhalenso mopitirira pamenepo poyerekeza ndi chuma chao. Popanda wina aliyense woŵakakamiza adatipempha, natiwumiriza kuti tiŵapatse mwai woti nawonso athandize anthu a Mulungu a ku Yudeya. Ndipo adathandizadi mopitirira pa zimene tidaayembekeza, pakuti poyamba adadzipereka kwa Ambuye, kenaka mwa kufuna kwa Ambuye adadziperekanso kwa ife. Nchifukwa chake tidaapempha Tito kuti akatsirizenso pakati panu ntchitoyi yakusonkhanitsa zopereka zachifundo imene iye anali atayamba kale. Zonse mudalandira pakulu, monga kukhulupirira, kulankhula, kudziŵa zinthu, kuchita changu pa zonse, ndiponso kutikonda. Motero tifuna kuti muperekenso pakulu zachifundozi. Pamene ndikunena zimenezi, sindikuchita kulamula ai. Pakukufotokozerani za changu cha ena, ndingofuna kuwona ngati chikondi chanu ndi chikondi chenicheni. Mukudziŵa kukoma mtima kwa Ambuye athu Yesu Khristu. Ngakhale anali wolemera, adakhala mmphaŵi chifukwa cha inu, kuti ndi umphaŵi wakewo inu mukhale olemera. Pa nkhani imeneyi maganizo anga ndi akuti nkwabwino kuti mutsirize zimene mudayamba kale chaka chathachi, osati kungofuna kuzichita, komanso kuzichita kumene. Tiyeni tsono muzitsirize. Paja munali ndi changu pofuna kuzichita, muchitenso changu tsopano kuzitsiriza molingana ndi zimene muli nazo. Malinga munthu akakhala ndi changu cha kupereka, Mulungu amalandira mokondwa zimene munthuyo ali nazo, ndipo samkakamiza kuti apereke zimene alibe. Sindikufuna kunena kuti inuyo muvutike, ena apepukidwe, ai, koma kuti pakhale kulingana. Poti inu muli ndi zambiri tsopano, muyenera kumathandiza osoŵa, kuti m'tsogolomo nawonso akadzakhala ndi zochuluka, azidzakuthandizani pa zosoŵa zanu. Motero padzakhala kulingana. Paja Malembo akuti, “Amene adapata zambiri, sizidamchulukire, amene adapata pang'ono, sizidamchepere.” Tiyamike Mulungu kuti adaika mumtima mwa Tito changu chomwecho chimene ife tili nacho pokuthandizani. Pakuti sadangochita zimene tidampempha, koma changu chake chinali chachikulu, kotero kuti adatsimikiza yekha zobwera kwanuko. Pamodzi ndi iyeyo tikutuma mbale wathu uja, amene mipingo yonse ikumuyamika chifukwa cha ntchito yake yolalika Uthenga Wabwino. Ndipo si pokhapo ai, komanso mipingo idamsankha kuti adzatiperekeze pokapereka zopereka zachifundozi. Tikukonza zimenezi kuti tichitire Ambuye ulemu, ndiponso kuti tiwonetse mtima wathu wofuna kuthandiza. Sitikufuna kupatsa anthu chifukwa choti azitinenera zoipa pa mayendetsedwe athu a zopereka zachifundo zochulukazi. Ifetu tikufuna kuchita zabwino, osati pamaso pa Ambuye pokha, komanso pamaso pa anthu. Pamodzi ndi iwowo tikutuma mbale wathu wina. Takhala tikumuyesa kaŵirikaŵiri, ndipo tampeza kuti ndi wachangu ndithu pa zinthu zambiri. Tsopano akufunitsitsa koposa kuti athandize, popeza kuti amakukhulupirirani kwambiri. Kunena za Tito, iyeyu ndi wantchito mnzanga amene amagwirizana nane pokuthandizani. Kunenanso za abale athu enawo, ngotumidwa ndi mipingo, ndipo Khristu amalemekezedwa chifukwa cha iwo. Tsono muŵatsimikizire chikondi chanu, kuti mipingo yonse ichiwone, ndi kudziŵa kuti sitikulakwa tikamakunyadirani. Nkosafunikira kuti ndikulembereni za zopereka zothandizira anthu a Mulungu a ku Yudeya. Ndikudziŵa kuti mumafunadi kuthandiza, ndipo ndimakunyadirani kwa anthu a ku Masedoniya chifukwa cha chimenechi. Ndimaŵauza kuti, “Abale a ku Akaiya adakonzeka kale chaka chatha kuti athandize.” Ndipo changu chanu chautsa ena ambiri. Koma ndikutuma abale athuŵa, kuti kukunyadirani kwathu pa zimenezi kusakhale kwachabe, koma kuti mukhaledi okonzeka monga momwe ndidaanenera. Ngati anthu ena a ku Masedoniya adzandiperekeze ndi kukupezani muli osakonzeka, tidzachita manyazi kwambiri kuti tinkakunyadirani pachabe, koma makamaka inuyo ndiye mudzachite manyazi kwambiri. Nchifukwa chake ndidaganiza kuti ndiyenera kupempha abale ameneŵa kuti abwere kwa inu ndisanafike ineyo, ndipo kuti akonzeretu mphatso imene mudalonjeza kale. Pamenepo mphatsoyo idzakhala yokonzekeratu, ndipo idzakhaladi mphatso yeniyeni, osati kanthu kamene mwapereka mokakamizidwa. Nkhanitu ndi iyi: wobzala pang'ono, adzakololanso pang'ono, wobzala zochuluka, adzakololanso zochuluka. Aliyense apereke monga momwe adatsimikiziratu mumtima mwake, osati ndi chisoni kapena mokakamizidwa, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwa. Mulungu angathe kukupatsani madalitso onse pakulu, kuti nthaŵi zonse mukhale ndi zokukwanirani inuyo, ndipo zinanso zochuluka kuti mukathandize pa ntchito zonse zabwino. Za munthu wotere paja Malembo akuti, “Wapereka mphatso zake moolowa manja kwa anthu osauka. Chilungamo chake nchamuyaya.” Mulungu amene amapatsa mbeu kwa wobzala, ndiponso chakudya choti adye, adzakupatsani mbeu zoti mubzale, ndipo adzazichulukitsa. Adzachulukitsanso zipatso zake za chifundo chanu. Adzakulemeretsani pa zonse, kuti mukhale oolowa manja ndithu, kotero kuti ambiri adzathokoza Mulungu chifukwa cha mphatso yanu imene tiŵatengereko. Zoonadi ntchito imeneyi yomwe mukuchitira anthu a Mulungu, siingoŵathandiza pa zosoŵa zao, komanso chotsatira chake china nchakuti anthu ochuluka adzathokoza Mulungu kwambiri. Pakuti ntchito imeneyi ikuŵatsimikizira kuti chifundo chanu nchoona, iwo adzatamanda Mulungu chifukwa cha kumvera kwanu povomereza Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Adzatero chifukwanso cha ufulu wanu poŵagaŵirako iwowo ndi anthu ena onse zinthu zimene muli nazo. Tsono adzakuwonetsani chikondi chao ndi kukupemphererani, chifukwa Mulungu wakukomerani mtima kopitirira. Tiyamike Mulungu chifukwa cha mphatso yake yosaneneka. M'dzina la Yesu Khristu wa mtima woleza ndi wofatsa, ine Paulo mwiniwake, amene anthu ena amati ndine wamantha pamene ndili pamaso panu, koma wosaopa konse pamene ndili nanu kutali, ndikuti mundimve. Ndikukupemphani kuti ndikadzafika kwanuko ndisadzakakamizidwe kudzudzula mosaopa konse anthu amene akuti machitidwe athu ndi otsata za anthu chabe. Ndi zoona kuti ndife anthu, koma sitimenya nkhondo motsata za anthu chabe. Pakuti zida zathu zakhondo si za anthu chabe, koma ndi mphamvu zochokera kwa Mulungu zotha kuwononga malinga. Timagonjetsa maganizo onyenga, ndiponso kudzikuza kulikonse koletsa anthu kudziŵa Mulungu. Timagonjetsa ganizo lililonse kuti limvere Khristu. Ndipo inu mutakhala omvera kwenikweni, tili okonzeka kulanga aliyense amene samvera. Ganizani bwino pa zimene mukuwona ndi maso anu. Kodi pali wina amene amakhulupirira kuti ndi wake wa Khristu? Chabwino, koma akumbukire kuti monga iye ali wake wa Khristu, ifenso ndife ake a Khristu. Ndipotu ngakhale mwina ndikunyadira mokakata ulamuliro umene Ambuye adatipatsa woti tikulimbitse nawoni, osati kukuwonongani ai, ndithu sindidzachita manyazi. Tsono musayese kuti ndikungokuwopsezani ndi makalata anga. Paja ena amati, “Makalata a Paulo ngaukali ndi amphamvu, koma mwiniwake akakhala pakati pathu, iyeyo ngwofooka ndipo mau ake ndi achabe.” Anthu oganiza zotere, adziŵe kuti palibe kusiyana pakati pa zimene timanena m'makalata pamene tili nanu kutali ndi zimene timachita tikakhala nanu pamodzi. Sikuti timayesa kudzilinga kapena kudziyerekeza ndi ena amene amadzichitira okha umboni. Amapusa chabe pakungodziyesa ndi muyeso waowao, ndi kudzilinganiza ndi anzao a m'gulu lao lomwe. Kunena za ife, sitinganyade mopitirira malire. Tidzasamala malire omwe Mulungu adatiikira potifikitsa mpaka kwa inu. Sitidabzole malire athu, monga ngati sitidakafike kwanu. Tinali oyamba ndife kukafika kwanu ndi kulalika Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Motero sitinyadira ntchito zimene anthu ena adazigwira m'dera limene Mulungu adatiikira ife. Kwenikweni tikuyembekeza kuti chikhulupiriro chanu chidzakula, ndipo kuti ntchito yathunso pakati panu idzakula, koma osabzola malire a dera lathu. Pambuyo pake tingathe kukubzolani nkukalalika Uthenga Wabwino ku maiko enanso, osanyadira ntchito imene munthu wina wachita kale m'dera lake. Paja Malembo akuti, “Wofuna kunyada, anyadire Ambuye.” Pakuti munthu wovomerezeka, si amene amadzichitira yekha umboni, koma amene Ambuye amamchitira umboni. Ndikadakonda kuti mundilekerere pang'ono pa kupusa kwangaku. Tandilekereranipo ndithu. Nsanje imene ndikukuchitirani ndi yonga ya Mulungu. Pakuti ndidakupalitsani ubwenzi ndi mwamuna mmodzi yekha, ngati namwali wangwiro ndi woyera mtima, kuti mukhale akeake a Khristu. Njoka ndi kuchenjera kwake idanyenga Heva. Ndikuwopa kuti maganizo anu angaipitsidwe chimodzimodzi, ndipo mungaleke kudzipereka kwa Khristu ndi mtima wonse. Wina amati akabwera kudzalalika Yesu wina wosiyana ndi amene tidamlalika ife, inu mumangomulekerera. Kapena mukalandira mzimu wina wosiyana ndi Mzimu Woyera amene mudamlandira kale, inu nkumaloladi. Mwinanso mukalandira Uthenga Wabwino wosiyana ndi umene mudalandira kale, inu nkumauvomeradi msangamsanga. Ndikuganiza kuti atumwi anu apamwambawo sandiposa ine pa kanthu kalikonse. Ngakhale ndine mbuli pa luso lolankhula, koma pa nzeru ndiye ai. Zimenezi ndidakuwonetsani kaŵirikaŵiri pa zonse. Ndidadzitsitsa ndekha ineyo, kuti inu mukule. Ndidakulalikirani mwaulere Uthenga Wabwino wa Mulungu. Kodi ndiye kuti pakutero ndidalakwa? Pakulandira zondithandiza kuchokera ku mipingo ina, ndidachita ngati kuŵalanda zao kuti ndikutumikireni inu. Ndipo pamene ndinali kwanuko, nditasoŵa kanthu, sindidavute aliyense, pakuti abale ena ochokera ku Masedoniya adaandipatsa zonse zimene ndinkasoŵa. Pa zonse ndinkasamala kwambiri kuti ndisakhale ngati katundu wokulemerani, ndipo ndidzapitirirabe kutero. Malinga ndi choona cha Khristu chimene chili mwa ine, ndikunenetsa kuti palibe munthu amene adzandiletsa kunyadira zimenezi m'madera onse a ku Akaiya. Ndikutero chifukwa chiyani? Kodi monga sindikukondani? Akudziŵa ndi Mulungu kuti ndimakukondani. Zimene ndikuchita tsopano, ndidzazichitabe, kuti ndisaŵapatse mpata onyenga aja amene akufuna danga loti anyadire, ndi kumanena kuti iwonso akugwira ntchito molingana ndi ife. Anthu otereŵa si atumwi oona, koma antchito onyenga, amene amadzizimbaitsa, naoneka ngati atumwi a Khristu. Zimenezitu si zododometsa ai, pakuti Satana yemwe amadzizimbaitsa, naoneka ngati mngelo wounikira anthu. Motero si chodabwitsa ngati atumiki ake omwe amadzizimbaitsa, naoneka ngati otumikira chilungamo. Potsiriza adzalandira molingana ndi zimene ankachita. Ndikufuna kubwerezanso kuti munthu wina aliyense asandiyese wopusa. Koma ngati inuyo mukundiyesadi wopusa, chabwino mundilandire ngati chitsiru, kuti inenso ndinyadirepo. Zimene ndimati ndinena panozi si zimene Ambuye afuna kuti ndinene, koma ndikungonyada, monga momwe amachitira wopusa. Tsono popeza kuti ambiri akunyadira zapansipano, inenso ndidzatero. Inu mumati ndinu anzeru kwambiri, nchifukwa chake anthu opusa mumangoŵalekerera mokondwa. Mumangolekerera munthu akakuyesani akapolo, kapena akadya chuma chanu, kapena akakunyengani, kapena akakunyozani, kapena akakumenyani kumaso. Ndikuvomera mwamanyazi kuti ife sitinali olimba mtima kuti nkuchita zotere. Tsopano ndilankhula ngati wopusa: zimene wina aliyense anganyadire, zomwezo inenso ndingathe kuzinyadira. Kodi iwo ndi Ahebri? Inenso. Kodi iwo ndi Aisraele? Inenso. Kodi iwo ndi ana a Abrahamu? Inenso. Kodi iwo ndi atumiki a Khristu? Ndikulankhula ngati wamisala, ndine mtumiki woposa iwowo. Ndidagwira ntchito kwambiri kopambana iwo, kaŵirikaŵiri ndinali pafupi kufa. Kasanu Ayuda adandikwapula mikwapulo 39. Katatu Aroma adandimenya ndi ndodo. Kamodzi anthu adandiponya miyala. Katatu pa maulendo athu apanyanja, chombo chathu chidasweka. Nthaŵi ina ndidayandama pakati pa nyanja tsiku lathunthu, usana ndi usiku. Pa maulendo anga ochuluka ndidakumana ndi zoopsa za mitsinje, zoopsa za achifwamba, zoopsa zochokera kwa Ayuda anzanga, ndi zina zochokera kwa akunja. Ndidapeza zoopsa m'mizinda, m'thengo, ndi pakati pa abale onyenga. Ndidagwira ntchito zolemetsa, ndipo kaŵirikaŵiri sindidalaŵe tulo. Ndidamva njala ndi ludzu, kaŵirikaŵiri osaona chakudya, ndipo kusoŵa zovala ndi kuzizidwa. Kuwonjezera pa zonsezi, tsiku ndi tsiku ndimapsinjidwa ndi udindo wa kusamalira mipingo yonse. Ndani ali wofooka, ine osakhala naye pamodzi m'kufooka kwakeko? Ndani amene mnzake amchimwitsa, ine osavutika mu mtima? Ngati ndiyenera kunyada, ndidzanyadira kufooka kwanga. Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu, amene tiyenera kumtamanda nthaŵi zonse, akudziŵa kuti sindikunama. Pamene ndinali ku Damasiko, bwanamkubwa woimirira mfumu Areta, adaaika alonda kuzinga mzinda wonsewo kuti andigwire. Koma anthu adandiika m'dengu nanditsitsira pa windo la m'lingalo, motero ndidamthaŵira. Ndiyenera kunyada, tsono kunyada kwake nkopanda phindu. Komabe ndimati ndikambe za zimene Ambuye adandiwonetsa m'masomphenya, ndiponso za zimene adandiwululira. Ndikudziŵa mkhristu wina amene adaatengedwa mwadzidzidzi kupita Kumwambamwamba. Papita zaka khumi ndi zinai chichitikire cha zimenezi. Sindidziŵa ngati zidaachitika ali m'thupi kapena ali kunja kwa thupi. Akudziŵa ndi Mulungu zimenezi. Ndikudziŵa kuti munthuyo adaatengedwa mwadzidzidzi kupita ku Paradizo. Sindikudziŵa ngati zimenezi zidaachitika ali m'thupi, kapena ali kunja kwa thupi. Akudziŵa ndi Mulungu zimenezi. Kumeneko munthuyo adamva zinthu zosasimbika, zinthu zimene munthu sangazilankhule. Munthu wotere ndidzamnyadira, koma kunena za ine ndekha, sindidzanyadira kanthu kena koma kufooka kwanga kokha. Ndikadafuna kunyada, sindikadakhala ngati wopusa, chifukwa ndikadalankhula zoona zokha. Koma sindidzanyada, kuwopa kuti wina aliyense angandiyese wopambana, kusiyana ndi m'mene amandiwonera, ndiponso ndi m'mene amandimvera ndikamalankhula. Koma kuwopa kuti ndingamadzitukumule chifukwa cha zazikulu kwambiri zimene Ambuye adandiwululira, Mulungu adandipatsa cholasa ngati minga m'thupi. Adalola wamthenga wa Satana kuti azindimenya, kuti ndingamanyade kwambiri. Pamenepo ndidapempha Ambuye katatu kuti andichotsere chimenechi, koma Iwo adandiwuza kuti, “Chithandizo changa nchokukwanira. Mphamvu zanga zimaoneka kwenikweni mwa munthu wofooka.” Nchifukwa chake makamaka ndidzanyadira kufooka kwanga, kuti mphamvu za Khristu zikhale mwa ine. Tsono ndimakondwera pamene ndili wofooka, pamene anthu andinyoza, namandizunza, ndiponso pamene ndimva zoŵaŵa ndi kusautsidwa chifukwa cha Khristu. Pakuti pamene ndili wofooka, mpamene ndili ndi mphamvu. Ndasanduka wopusa, koma ndinu mwandichititsa zimenezi. Ndinu mukadayenera kundichitira umboni. Pakuti ngakhale sindili kanthu, atumwi anu apamwamba aja sandipambana pa kanthu kalikonse. Ndidakutsimikizirani mopirira kwambiri kuti ndine mtumwi, pakuchita pakati panu zizindikiro, zozizwitsa ndi ntchito zina zamphamvu. Kodi nchiyani chimene ndidachitira mipingo ina, inu osakuchitirani, kupatula chokhachi chakuti sindidakhale ngati katundu wokulemetsani? Ndikhululukireni kulakwa kwangaku. Aka nkachitatu tsopano kukonzeka kuti ndibwere kwanuko, ndipo sindidzakhala ngati katundu wokulemetsani. Sindikufuna zinthu zanu, koma ndikufuna inuyo. Pakuti si udindo wa ana kusungira makolo ao chuma, koma ndi udindo wa makolo kusungira ana ao chuma. Kunena za ine, ndidzakondwa kupereka zanga zonse, ndi kutaya ngakhale moyo wanga womwe chifukwa cha inu. Ine ndikamakukondani kwambiri chotere, kodi ndiye kuti inuyo muzingondikonda pang'ono? Momwemo tsono, mudzandivomereza kuti ine sindidakhale ngati katundu wokulemetsani. Koma kapena wina adzati popeza kuti ndine wochenjera, ndidakuchenjeretsani. Kodi kapena ndidakuchenjererani mwa aliyense amene ndidamtuma kwa inu? Ndidapempha Tito kuti apite, kenaka ndidatuma mbale wathu wina pamodzi naye. Kodi Titoyo adakuchenjererani? Kodi suja iye ndi ine tinkachita zonse ndi mtima umodzi? Suja tinkatsata njira imodzimodzi? Kapena mwakhala mukuganiza kuti tikuyesa kudziteteza pamaso panu. Iyai, koma pokhala pamaso pa Mulungu, timalankhula mwa Khristu, ndipo pa zonsezi, okondedwa anga, timangofuna kukulimbitsani mtima. Ndikuwopa kuti ndikadzabwera kwanuko, mwina nkudzakupezani muli osiyana ndi m'mene ndikadafunira. Ndikuwopa kuti mwina inunso nkudzandipeza ine wosiyana ndi m'mene mukadafunira. Ndikuwopanso kuti mwina ine nkudzapeza kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusinjirirana, ugogodi, kudzitukumula, ndiponso chisokonezo. Ndikuwopa kuti ndikadzabweranso kwanuko, mwina Mulungu wanga nkudzandinyazitsa pamaso panu, ineyo nkudzalira misozi chifukwa cha ambiri amene adachimwa kale, ndipo sadalape zonyansa zao, dama lao, ndi mayendedwe ao oipa. Aka nkachitatu tsopano kuti ndibwere kwanuko. Mau a Mulungu akuti, “Mlandu uliwonse uzitsimikizika ndi umboni wa anthu aŵiri kapena atatu.” Inu amene mudaachimwa kale, ndiponso ena onse, paja ndidaakuuzani pamene ndinali kwanuko kachiŵiri kaja ndipo ndikubwereza kukuuziranitu tsopano ndisanafike, kuti ndikadzabweranso, sindidzamchitira chifundo wina aliyense. Pamenepo mudzaona chitsimikizo chimene mukufuna chakuti Khristu amalankhula kudzera mwa ine. Iyeyu sali wofooka pa zimene amachita nanu, koma amaonetsa mphamvu zake pakati panu. Anali wofooka pamene adapachikidwa pa mtanda, komabe tsopano ali moyo mwa mphamvu ya Mulungu. Ifenso ndife ofooka mwa Iye, koma tidzakhala amoyo pamodzi naye ndi mphamvu ya Mulungu, pogwira ntchito yathu pakati panu. Muzidziyesa nokha inuyo kuti mutsimikize ngati mukusungadi chikhulupiriro chanu. Muzidzifunsitsa nokha. Simudziŵa nanga kuti Yesu Khristu ali mwa inu? Ngati si choncho, mwalephereratu. Koma ndikhulupirira kuti mudzazindikira kuti ife sitidalephere. Tikupempha Mulungu kuti musachite choipa chilichonse. Osati kuti ife tiwoneke ngati opambana, koma kuti inu muchite zimene zili zoyenera, ngakhale ife tiwoneke ngati talephera. Pakuti sitingathe kuchita chilichonse chotsutsana ndi choona, koma zokhazokha zothandizira choonacho. Timakondwa pamene ife tili ofooka koma inu muli amphamvu. Chimene tikupempha Mulungu nchakuti mudzasanduke angwiro. Ndikulemba zimenezi ndisanafike kwanu, kuti ndikadzafika, pasadzakhale chifukwa choti ndidzagwiritse ntchito ulamuliro wanga mwaukali. Ambuye adandipatsa ulamulirowo kuti ndilimbitse mpingo, osati kuti ndiupasule. Tsono abale, kondwani. Mverani zimene ndikukulangizani, ndipo mukonze zimene zidalakwika. Muzimvana ndi kukhala mu mtendere. Pamenepo Mulungu wachikondi ndi wamtendere adzakhala nanu. Mupatsane moni mwa chikondi choona. Anthu onse a Mulungu akukupatsani moni. Madalitso a Ambuye Yesu Khristu ndi chikondi cha Mulungu ndiponso chiyanjano cha Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse. Ndine, Paulo, mtumwi. Adandisankha si anthu ai, koma Yesu Khristu, ndiponso Mulungu Atate amene adamuukitsa kwa akufa. Ineyo pamodzi ndi abale onse amene ali nane, tikulembera mipingo ya ku Galatiya. Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere. Khristuyo adadzipereka chifukwa cha machimo athu, kuti atipulumutse ku njira za moyo woipa uno. Pakutero adachita zimene Mulungu Atate athu ankafuna. Ulemu ukhale kwa Mulunguyo mpaka muyaya. Amen. Ndikudabwa kuti mukupatuka msangamsanga motere, kusiya Mulungu amene adakuitanani mwa kukoma mtima kwa Khristu, ndipo kuti mukutsata uthenga wabwino wina. Koma palibe konse uthenga wabwino wina. Pali anthu ena amene akukusokonezani, ndipo akufuna kupotoza Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Koma aliyense, kaya ndife kaya ndi mngelo wochokera Kumwamba, akakulalikirani uthenga wabwino wosiyana ndi uja tidakulalikiraniwu, ameneyo akhale wotembereredwa. Ndikubwereza kunena zimene tidaanenanso kale, kuti munthu aliyense akakulalikirani uthenga wabwino wosiyana ndi Uthenga Wabwino umene mudalandira uja, iyeyo akhale wotembereredwa. Kodi ponena zimenezi ndiye kuti ndikufuna kuti anthu andivomereze? Iyai, koma kuti andivomereze ndi Mulungu. Kodi ndikuyesa kukondweretsa anthu? Ndikadayesabe kukondweretsa anthu, si bwenzi ndilinso mtumiki wa Khristu. Abale, ntakuuzani: Uthenga Wabwino umene ine ndimalalika, ndi wosachokera kwa anthu. Sindidaulandire kwa munthu, ndipo palibenso munthu amene adandiphunzitsa Uthengawo, koma ndi Yesu Khristu yemwe amene adawuulula kwa ine. Mudamva za mayendedwe anga kale pamene ndinali m'Chiyuda. Ndinkazunza Mpingo wa Mulungu koopsa, ndipo ndinkayesetsa kuuwonongeratu. Ndinkapambana anzanga ambiri a msinkhu wanga pochita zachiyuda, ndipo ndinali wachangu koposa potsata miyambo ya makolo athu. Koma Mulungu adandipatula ndisanabadwe, ndipo mwa kukoma mtima kwake adandiitana. Tsono pamene adatsimikiza zondiwululira Mwana wake, kuti choncho ndikalalike Uthenga Wabwino wonena za Iye kwa anthu amene sali Ayuda, sindidapite kwa munthu aliyense kuti ndikapemphe nzeru. Sindidapite ngakhalenso ku Yerusalemu kwa anthu amene anali atumwi kale ine ndisanakhale mtumwi. Koma ndidapita ku Arabiya kenaka nkubwereranso ku Damasiko. Pambuyo pake, patapita zaka zitatu, ndidapita ku Yerusalemu kukacheza ndi Petro, ndipo ndidangokhala naye masiku khumi ndi asanu. Sindidaonenso mtumwi wina aliyense kupatula Yakobe yekha, mbale wa Ambuye. Ndikulumbira pamaso pa Mulungu kuti zimene ndikukulemberanizi ndi oona, sindikunama ai. Pambuyo pake ndidakafika ku madera a ku Siriya ndi a ku Silisiya. Koma chonsecho nkuti mipingo yachikhristu ya ku Yudeya isanandiwone ndi kundidziŵa bwino. Inali itangomva mbiri chabe yakuti, “Munthu uja ankatizunza kaleyu, tsopano akulalika chikhulupiriro chimene kale lija ankayesetsa kuchiwononga.” Motero mipingoyi inkalemekeza Mulungu chifukwa cha ine. Pambuyo pake, patapita zaka khumi ndi zinai, ndidapitanso ku Yerusalemu pamodzi ndi Barnabasi. Ndidatenganso Tito kuti apite nafe. Ndidapita kumeneko chifukwa Mulungu adaachita kundiwululira kuti ndipite. Mu msonkhano wa atsogoleri okhaokha ndidaŵafotokozera Uthenga Wabwino umene ndimalalika pakati pa anthu osakhala Ayuda. Ndidachita zimenezi kuwopa kuti ntchito imene ndikuchitayi, ndiponso imene ndidachita kale, ingakhale yachabe. Koma mnzanga uja, Tito, ngakhale ndi Mgriki, sadamkakamize kuti aumbalidwe, ngakhale kuti anthu ena adaafuna kuti iyeyu aumbalidwe ndithu. Anthu ameneŵa adaabwera modzizimbayitsa ngati abale athu. Iwowo adangodzaloŵa ngati azondi kuti adzaone ufulu wathu umene tili nawo mwa Khristu Yesu. Ankafuna kutisandutsa akapolo. Sitidaŵagonjere mpang'ono pomwe, popeza kuti tinkafuna kukusungirani kwathunthu zoona za Uthenga Wabwino. Koma kunena za aja ankaŵayesa atsogoleriŵa, (kaya analidi atsogoleri kaya, ndilibe nazo kanthu. Mulungu sakondera paja), iwowo sadaonjeze kanthu kena koti ndilalike. Makamaka adaaona kuti Mulungu adandipatsa ine ntchito ya kulalika Uthenga Wabwino kwa anthu osakhala Ayuda, monga momwe adapatsira Petro ntchito ya kuulalika kwa Ayuda. Pakuti Mulungu yemweyo amene adagwira ntchito mwa Petro pomutuma ngati mtumwi kwa Ayuda, adagwiranso ntchito mwa ine, pondituma ngati mtumwi kwa anthu a mitundu ina. Yakobe, Petro ndi Yohane, amene anthu ankaŵaona kuti ndi mizati mu Mpingo, adazindikira kuti ineyo Mulungu adandipatsadi ntchito imeneyi. Motero adagwirana chanza ndi ine ndiponso ndi Barnabasi, kutsimikiza chiyanjano chathu. Ndipo tidavomerezana kuti ine ndi Barnabasi tipite kwa anthu a mitundu ina, iwowo apite kwa Ayuda. Adangopempha chokhachi kuti tisaleke kukumbukira anthu ao aumphaŵi. Ndipotu chimenechi ndicho ndakhala ndikuchita moikapo mtima. Koma pamene Petro adafika ku Antiokeya, ndidamtsutsa poyera, chifukwa adaapezeka wolakwadi. Pakuti asanafike anthu ena amene Yakobe adaaŵatuma, iye ankadya pamodzi ndi abale osakhala Ayuda. Koma atafika iwowo, iye adayamba kudzipatula, osafuna kudya nawonso, chifukwa choopa anthu amene ankafuna kuti omwe sali Ayuda aumbalidwe. Abale ena onse ochokera ku Chiyuda nawonso adayamba kuchita chiphamaso, kotero kuti ngakhale Barnabasi yemwe adaatengeka nacho chiphamaso chaocho. Ine ndidaaona kuti iwo sakuyenda molunjika, sakutsata choona cha Uthenga Wabwino. Tsono ndidauza Petro pamaso pa onse kuti, “Iwe ndiwe Myuda, komabe ukukhala ngati munthu wa mtundu wina, osati Myuda. Nanga ungakakamize bwanji anthu a mitundu ina kukhala ngati Ayuda?” Ife ndife a mtundu wa Ayuda, osati anthu aja amati akunja ochimwa. Komabe tikudziŵa kuti munthu sangapezeke kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu pakuchita ntchito zolamulidwa ndi Malamulo, koma pakukhulupirira Yesu Khristu. Ifenso tidakhulupirira Khristu Yesu kuti tisanduke olungama pamaso pa Mulungu pakukhulupirira Khristu, osati chifukwa cha ntchito zolamulidwa ndi Malamulo. Pakuti palibe munthu amene angapezeke kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu chifukwa cha ntchito zolamulidwa ndi Malamulo. Tsono ngati ifeyo, poyesetsa kusanduka olungama mwa Khristu, tikupezeka kuti ndifenso ochimwa, kodi pamenepo ndiye kuti Khristu ndi wotumikira uchimo? Mpang'ono pomwe. Ngati ndimanganso zomwezo zimene ndidaagamula, pamenepo kukuwonekeratu kuti ndine wopalamula. Malamulo ndiwo adandizindikiritsa kuti ndiyenera kulekeratu kuŵadalira Malamulowo, ndipo kuti moyo wanga wonse uyenera kukhala wodalira Mulungu mwini. Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine. Sindiisandutsa yopandapake mphatso yaulere ya Mulungu. Pakuti ngati munthu atha kusanduka wolungama pamaso pa Mulungu pakutsata Malamulo, ndiye kuti Khristu adafa pachabe. Agalatiya opusa inu, adakulodzani ndani? Pamene tidakulalikirani Yesu Khristu, tidamuwonetsa poyera pamaso panu ngati wopachikidwa pa mtanda. Ndikufunseni chinthu chimodzi chokha: Kodi mudalandira Mzimu Woyera pakutsata Malamulo, kapena pakumva ndi kukhulupirira Uthenga Wabwino? Kani ndinu opusa chotere? Kodi zimene Mzimu Woyera adayamba kuchita mwa inu, mukufuna kuzifikitsa pake penipeni tsopano ndi mphamvu zanuzanu? Kodi mudalandira zonse zija pachabe? Sindikukhulupirira kuti mpachabe. Kodi Mulungu amene amakupatsani Mzimu Woyera, nachita zozizwitsa pakati panu, amachita zimenezi chifukwa mumatsata Malamulo, kapena chifukwa mudamva ndi kukhulupirira Uthenga Wabwino? Paja ponena za Abrahamu Malembo akuti, “Iye adaakhulupirira Mulungu, motero Mulungu adamuwona kuti ngwolungama.” Muzindikire tsono kuti ndi anthu amene amakhulupirira omwe ali ana enieni a Abrahamu. Koma Malembo adaoneratu kuti anthu a mitundu ina pakukhulupirira, Mulungu adzaŵaona kuti ngolungama pamaso pake. Nchifukwa chake Malembowo adaauziratu Abrahamu Uthenga Wabwinowu wakuti, “Mwa iwe Mulungu adzadalitsa anthu a mitundu yonse.” Abrahamu adakhulupirira, ndipo Mulungu adamdalitsa. Motero pamodzi ndi Abrahamuyo Mulungu amadalitsanso onse okhulupirira. Onse amene amadalira ntchito za Malamulo ndi otembereredwa. Paja Malembo akuti, “Ndi wotembereredwa aliyense amene satsata zonse zolembedwa m'buku la Malamulo.” Komatu nchodziŵikiratu kuti palibe munthu amene angapezeke kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu pakuchita ntchito zolamulidwa ndi Malamulo. Paja Malembo akuti, “Munthu amene ali wolungama pamaso pa Mulungu pakukhulupirira, adzakhaladi ndi moyo.” Koma Malamulo akusiyana ndi chikhulupiriro, chifukwa Malembo akuti, “Munthu amene amachita zonse zolamulidwa ndi Malamulo, adzakhala ndi moyo pakutero.” Khristu adatiwombola ku temberero la Malamulo pakusanduka wotembereredwa m'malo mwathu. Paja Malembo akuti, “Ndi wotembereredwa aliyense wopachikidwa pa mtengo.” Khristu adachita zimenezi, kuti dalitso limene Mulungu adaalonjeza Abrahamu, lipatsidwe kwa anthu a mitundu yonse kudzera mwa Khristu Yesu, ndipo kuti pakukhulupirira tilandire Mzimu Woyera amene Mulungu adaatilonjeza. Abale, ndikufotokozereni zimenezi pokupatsani chitsanzo cha zimene zimachitika tsiku ndi tsiku. Anthu aŵiri akapangana natsimikiza chimodzi, palibe munthu angaphwanye panganolo kapena kuwonjezapo mau. Tsono Mulungu adapatsa malonjezo ake kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake. Sakunena kuti, “Ndi kwa mbeu zake” ai, ngati kuti akunena za anthu ambiri. Koma akunena kuti, “Ndi kwa mbeu yake”, popeza kuti akukamba za munthu mmodzi yekha. Ameneyu ndi Khristu. Chimene ndikunena ndi ichi: Mulungu adachita chipangano, nalonjeza kuchisunga. Malamulo a Mose, amene adadza patapita zaka 430, sangathe kuchiphwanya chipanganocho ndi kuwononga lonjezo la Mulungu lija. Mulungu akapatsa munthu madalitso chifukwa munthuyo ndi wotsata Malamulo, ndiye kuti madalitsowo sapatsidwanso chifukwa cha lonjezo ai. Koma Mulungu adadalitsa Abrahamu chifukwa adaalonjeza kutero. Nanga tsono cholinga cha Malamulo chinali chiyani? Mulungu adaonjezapo Malamulo kuti azindikiritse anthu machimo, mpaka mbeu ija ya Abrahamu, imene Mulungu adaaipatsa lonjezo lija, itabwera. Mulungu adapereka Malamulowo kudzera mwa angelo, ndiponso kudzera mwa munthu wochita ntchito ya mkhalapakati. Tsono tikati mkhalapakati, ndiye kuti pali anthu aŵiri. Koma Mulungu ali yekha. Kodi ndiye kuti Malamulo a Mose amatsutsana ndi malonjezo a Mulungu? Mpang'ono pomwe. Anthu akadalandira malamulo otha kuŵapatsa moyo, pamenepo bwenzi atasanduka olungama kudzera mwa malamulowo. Koma Malembo akunenetsa kuti zinthu zonse zili mu ulamuliro wa uchimo, kuti pakukhulupirira Yesu Khristu, anthu okhulupirira alandiredi zimene Mulungu adalonjeza. Chisanafike chikhulupirirochi, tinali ngati akaidi m'manja mwa Malamulo, kudikira kuti chikhulupiriro chimene chidaati chifikecho, chiwululidwe. Motero Malamulowo anali ngati namkungwi wathu, mpaka atabwera Khristu, kuti tisanduke olungama pamaso pa Mulungu pakukhulupirira. Popeza kuti tsopano chikhulupiriro chafika, namkungwiyo satilamuliranso. Nonsenu ndinu ana a Mulungu chifukwa mumakhulupirira Khristu Yesu. Pajatu nonsenu amene mudasanduka amodzi ndi Khristu pakubatizidwa, mudachita ngati kuvala moyo wa Khristu. Motero palibe kusiyana pakati pa Ayuda ndi anthu a mitundu ina, pakati pa akapolo ndi mfulu, kapenanso pakati pa amuna ndi akazi, pakuti nonsenu ndinu amodzi mwa Khristu Yesu. Ngati ndinu ake a Khristu, ndiye kuti ndinu ana a Abrahamu, oyenera kulandira zimene Mulungu adalonjeza. Chimene ndikufuna kunena ndi ichi: Mloŵachuma akali wamng'ono sasiyana ndi kapolo, ngakhale iyeyo ndi mwini chuma chonsecho. Mwanayo ayenera kumvera omulera ndiponso akapitao oyang'anira chuma chake, mpaka nthaŵi imene bambo wake adakhazikitsa. Chimodzimodzinso ifeyo, pamene tinali ana, tinali akapolo a miyambo yapansipano. Koma nthaŵi itakwana, Mulungu adatuma Mwana wake. Mwanayo adabadwa mwa mkazi, adabadwa woyenera kumvera Malamulo a Mose. Adachita zimenezi kuti akaombole amene anali akapolo a Malamulowo, ndipo kuti potero tisanduke ana a Mulungu. Pofuna kutsimikiza kuti ndinu ana ake, Mulungu adatitumizira Mzimu wa Mwana wake m'mitima mwathu, ndipo Mzimuyo amatinenetsa kuti, “Abba! Atate!” Motero sindiwenso kapolo ai, koma mwana. Ndipo popeza kuti ndiwe mwana wake, Mulungu adakusandutsanso mloŵachuma wake. Kale simunkadziŵa Mulungu, nchifukwa chake munkatumikira zomwe sizili milungu konse. Koma tsopano mukumdziŵa Mulungu, makamaka ndinene kuti Mulungu ndiye akudziŵa inu. Nanga bwanji mukubwereranso ku miyambo yachabe ndi yopanda phindu ija? Bwanji mukufuna kukhalanso akapolo ake? Mumasunga masiku, miyezi, nyengo ndi zaka. Ndikuwopa kuti mwinatu ntchito zanga zonse pakati panu ndidazigwira pachabe. Ndikukupemphani abale, musanduke ngati ine, pakuti inenso ndidasanduka ngati inu nomwe. Simudandilakwire konse. Monga mukudziŵa, pamene ndidayamba kukulalikirani Uthenga Wabwino, ndinkadwala. Ngakhale matendawo anali ngati mayeso kwa inu, komabe simudandinyoze kapena kunyansidwa nane. Kwenikweni mudandilandira ngati mngelo wa Mulungu, kapenanso ngati Khristu Yesu mwini. Nanga chimwemwe chanu chija chili kuti tsopano? Ndikukuchitirani umboni kuti nthaŵi imene ija, kukadatheka, mukadakolowola maso anu nkundipatsa ineyo. Monga ndasanduka mdani wanu popeza kuti ndakuuzani zoona? Anthu amene aja akuchita changu kwambiri pothandiza inu kuti akukopeni, koma changu chaocho sichili chabwino ai. Amangofuna kukupatutsani kuti muzichita changu pakuŵathandiza iwowo. Kwabwino nkumachita changu pa chinthu chabwino masiku onse, osati pokhapokha pamene ndili pamodzi nanu. Inu ana anga, monga mkazi amamva zoŵaŵa pochira, inenso ndikumva zoŵaŵa chifukwa cha inu mpaka moyo wa Khristu ukhazikike mwa inu. Ndikadakonda nditakhala nanu tsopano. Apo kapena ndikadasintha mau anga, chifukwa mwandithetsa nzeru. Inu ofuna kukhala akapolo a Malamulo, tandiwuzani. Kodi simukumvetsa zimene Malamulowo akunena? Paja Malembo akuti, Abrahamu anali ndi ana aamuna aŵiri: wina mai wake anali kapolo, winayo mai wake anali mfulu. Mwana amene mai wake anali kapolo uja, adabadwa monga momwe amabadwira ana onse. Koma mwana wina uja, amene mai wake anali mfulu, adabadwa chifukwa cha lonjezo la Mulungu. Zimenezi zili ngati fanizo. Akazi aŵiri aja akufanizira zipangano ziŵiri. Mmodzi (Hagara uja), ndi wochokera ku phiri la Sinai, ndipo ana ake amakhala akapolo. Hagarayo akufanizira phiri la Sinai la m'dziko la Arabiya, lofanizira Yerusalemu walero, amene ali m'ukapolo pamodzi ndi anthu ake onse. Koma Yerusalemu wakumwamba ndiye mfulu, ndipo ndiye mai wathu. Paja Malembo akuti, “Sangalala iwe chumba chosabala ana, imba nthungululu, fuula mokondwera, iwe amene sunamvepo zoŵaŵa za kubala. Ana a mkazi wosiyidwa ndi ochuluka koposa ana a mkazi amene ali naye mwamuna.” Tsono inu abale, ndinu ana a Mulungu chifukwa cha lonjezo lake, monga Isaki. Nthaŵi imeneyo mwana uja amene adaabadwa monga momwe amabadwira ana onseyu, ankasautsa mwana winayo wobadwa mwa mphamvu za Mzimu Woyera, ndipo mpaka tsopano zili chimodzimodzi. Nanga Malembo akuti bwanji? Akuti, “Mpirikitseni kapoloyu pamodzi ndi mwana wake. Mwana wa kapolo asadzakhale konse mloŵachuma pamodzi ndi mwana wa mfulu.” Nchifukwa chake, abale, ife sindife ana a kapolo, ndife ana a mfulu. Khristu adatimasula kuti tikhale mfulu ndithu. Muzichilimikira tsono, osalola kumangidwanso m'goli la ukapolo. Ndiye mvetsani, ine Paulo ndikukuuzani kuti mukalola kukuumbalani, Khristu simupindula nayenso konse ai. Ndikufuna kubwerezanso kuuza aliyense woumbalidwa, kuti ayenera kutsata Malamulo onse a Mose. Inu amene mukuyesa kusanduka olungama pakutsata Malamulowo, mudadzipatula nokha kusiya Khristu. Pamenepo mudalekana ndi madalitso aulere a Mulungu. Koma kunena za ife, chifukwa cha kulandira Mzimu Woyera ndiponso pakukhulupirira, tikuyembekeza kuti Mulungu adzatiwona kuti ndife olungama pamaso pake. Pakuti pamene tili mwa Khristu Yesu, kuumbalidwa kapena kusaumbalidwa kulibe kanthu, chachikulu nchakuti munthu akhale ndi chikhulupiriro chogwira ntchito mwachikondi. Munkathamanga bwino lomwe. Tsono adakuletsani ndani kuti musamverenso choona? Kukopeka kwanu kumeneku sikuchokera kwa Mulungu amene amakuitanani. Chofufumitsira chapang'ono chabe chimafufumitsa buledi yense. Ndili ndi chikhulupiriro mwa Ambuye, kuti simudzakhala ndi maganizo osiyana ndi anga. Koma amene akukusokonezaniyo, ngakhale akhale yani, Mulungu adzamlanga ndithu. Koma kunena za ine, abale, ngati ndikulalikabe kuti anthu aziwumbalidwa, nanga bwanji ndikuzunzidwabe? Ndikadalalikabe kuti anthu aziwumbalidwa, sibwenzi ndikuŵakhumudwitsa pakulalika mtanda wa Khristu. Ndikadakonda kuti amene akukuvutaniwo angodzithena basi. Inu abale, Mulungu adakuitanani kuti mukhale mfulu. Koma chenjerani kuti ufulu wanu umenewu usapatse mpata khalidwe lanu lokonda zoipa. Kwenikweni muzitumikirana mwachikondi. Paja Malamulo onse a Mulungu amaundidwa mkota pa lamulo limodzi lija lakuti, “Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.” Koma ngati muyamba kulumana ndi kukadzulana, muchenjere kuti mungaonongane kotheratu. Chimene ndikufuna kunena ndi ichi: Mulole Mzimu Woyera kuti azikutsogolerani. Mukatero, pamenepo simudzachita zimene khalidwe lanu lokonda zoipa limalakalaka. Pakuti khalidwelo limalakalaka zotsutsana ndi zimene Mzimu Woyera afuna, ndipo zimene Mzimu Woyera afuna zimatsutsana ndi zimene khalidwe lokonda zoipalo limafuna. Ziŵirizi zimadana, kotero kuti simungachite zimene mufuna kuchita. Koma ngati Mzimu Woyera akutsogolerani, ndiye kuti sindinunso akapolo a Malamulo a Mose. Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa, kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko, dumbo, kuledzera, kudakwa pa maphwando achipembedzo, ndi zina zotere. Ndikukuchenjezani tsopano, monga ndidaachitanso kale, kuti anthu amene amachita zotere, sadzalandirako Ufumu wa Mulungu. Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa. Amene ali ake a Khristu Yesu, adalipachika pa mtanda khalidwe lao lokonda zoipa, pamodzi ndi zokhumba zake ndi zilakolako zake. Ngati Mzimu Woyera adatipatsa moyo, tilolenso kuti Mzimu yemweyo azititsogolera. Tisakhale odzitukumula, oputana, kapena ochitirana dumbo. Abale, wina akagwa m'tchimo lililonse, inu amene Mzimu Woyera amakutsogolerani, mumthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe ndi zoipa. Muzithandizana kusenza zokulemetsani, ndipo pakutero mumvere ndithu lamulo la Khristu. Ngati munthu adziyesa kanthu, pamene chikhalirecho sali kanthu konse, amangodzinyenga. Aliyense aziyesa yekha ntchito zake m'mene ziliri. Ngati zili bwino, adzatha kunyadira chifukwa cha ntchito zake zokhazo, osati chifukwa zapambana ntchito za mnzake. Pakuti aliyense adzayenera kudzisenzera katundu wakewake. Munthu amene akuphunzira mau a Mulungu, agaŵireko mphunzitsi wake zabwino zonse zimene iye ali nazo. Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo. Munthu wongodalira zilakolako zake zokha, chimene adzakolole ndi imfa. Koma munthu wodalira Mzimu Woyera, chimene adzakolole ndi moyo wosatha. Tisatope nkuchita zabwino, chifukwa pa nthaŵi yake tidzakolola, ngati sitilefuka. Nchifukwa chake tsono, nthaŵi zonse tikapeza mpata, tizichitira anthu onse zabwino, makamaka abale athu achikhristu. Onani malemba akuluakulu amene ndikulemba ndi dzanja langalanga tsopano. Onse amene afuna kuti akome pamaso pa anthu, akukukakamizani kuti muumbalidwe. Ali ndi cholinga chimodzi chokha, chakuti asazunzidwe chifukwa cha mtanda wa Khristu. Pakuti ngakhale iwo omwe amene amaumbalidwa satsata Malamulo, komabe amafuna kuti inu muumbalidwe, kuti athe kunyadira kuumbalidwa kwanuko. Koma ine sindinganyadire kanthu kena kalikonse, koma mtanda wa Ambuye athu Yesu Khristu basi. Popeza kuti Iye adafa pa mtanda, tsopano zapansipano kwa ine zili ngati zakufa, ndipo inenso kwa zapansipano, ndili ngati wopachikidwa. Kuumbalidwa si kanthu, kusaumbalidwa si kanthunso, chachikulu nchakuti Mulungu apatse munthu moyo watsopano. Mulungu aŵapatse mtendere, ndipo aŵachitire chifundo anthu a Mulungu onse amene amatsata njira imeneyi. Kuyambira tsopano asandivutenso munthu wina aliyense, pakuti zipsera zimene ine ndili nazo pa thupi langa, zikutsimikiza kuti ndine wakewake wa Yesu. Abale, Ambuye athu Yesu Khristu akudalitseni inu nonse. Amen. Ndine, Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa kufuna kwa Mulungu. Ndikulembera anthu a Mulungu amene ali ku Efeso, amenenso ali okhulupirika mwa Khristu Yesu. Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere. Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Mwa Khristu Iye adatipatsa madalitso onse auzimu Kumwamba. Mulungu asanalenge dziko lapansi, adatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale oyera mtima ndi opanda cholakwa pamaso pake. Chifukwa chotikonda, adakonzeratu kuti mwa Yesu Khristu atilandire ngati ana ake. Adachita zimenezi chifukwa adaafuna kutero mwa kukoma mtima kwake. Adaafuna kuti tizitamanda ulemu wake chifukwa adatikomera mtima kopambana, pakutipatsa Mwana wake wokondedwa ngati mphatso yaulere. Ndi imfa ya Mwana wakeyo Mulungu adatipulumutsa, adatikhululukira machimo athu. Nzazikuludi mphatso zaulere zimene Mulungu adatipatsa mochuluka. Mwa luntha ndi nzeru adatiwululira chifuniro chake chimene kale chinali chobisika. Zimene adaati achite mwa kukoma mtima kwake ndi zomwe Iye mwini adaakonzeratu kale. Chimene Mulungu adalongosola kuti achite itakwana nthaŵi, nchakuti asonkhanitse pamodzi mwa Khristu zinthu zonse za Kumwamba ndi zapansipano. Paja Mulungu amaongolera zinthu zonse monga momwe Iye wafunira ndi m'mene watsimikizira. Iye adatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale akeake. Adazikonzeratu kuti ziyenera kukhala choncho. Adafuna kuti ife, amene tinali oyamba kuyembekeza Khristu, tilemekeze ulemerero wake. Mwa Khristu, inunso mutamva mau oona, amene ali Uthenga Wabwino wokupulumutsani, mudaukhulupirira. Nchifukwa chake Mulungu adakusindikizani chizindikiro chotsimikizira kuti ndinu akedi, pakukupatsani Mzimu Woyera amene Iye adaalonjeza. Mzimu Woyerayo ndiye chikole chotsimikizira kuti tidzalandiradi madalitso onse amene Mulungu adalonjeza kupatsa anthu ake, ndipo kuti Mulungu adzapulumutsa kwathunthu anthu amene adaŵaombola kuti akhale ake enieni. Cholinga cha zonsezi ndi chakuti tilemekeze ulemerero wake. Ndamva kuti mukukhulupirira Ambuye Yesu, ndiponso kuti mumakonda anthu a Mulungu. Nchifukwa chake sindilekeza kuthokoza Mulungu chifukwa cha inu. Ndimakukumbukirani m'mapemphero anga, ndipo ndimapemphera kuti Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu, Atate aulemerero, akuninkheni Mzimu Woyera, amene adzakupatsani nzeru, nadzaulula Mulungu kwa inu, kuti mumdziŵe kwenikweni. Ndimapemphera kuti Mzimu Woyerayo akuunikireni m'mitima mwanu, kuti mudziŵe zimene mungathe kuyembekezera kwa Mulungu amene adakuitanani. Ndimafunanso kuti mudziŵe kukula kwake kwa ulemerero ndi madalitso amene Mulungu amalonjeza kupatsa anthu ake. Ndiponso ndikufuna kuti mudziŵe mphamvu yake yopitirira muyeso imene ikugwira ntchito mwa ife omkhulupirira. Mphamvuyi ndi yomwe ija yolimba koposa, imene Mulungu adaigwiritsa ntchito pamene adaukitsa Khristu kwa akufa, namkhazika ku dzanja lake lamanja m'dziko la Kumwamba. Adamkhazika pamwamba pa mafumu onse, aulamuliro onse ndi akuluakulu onse a Kumwamba, ndiponso pamwamba pa maina ena onse amene anthu angaŵatchule nthaŵi ino kapenanso nthaŵi ilikudza. Mulungu adagonjetsa zonse kuti zikhale pansi pa mapazi a Khristu, ndipo adamkhazika pamwamba pa zonse kuti akhale mutu wa Mpingo. Mpingowu ndi thupi la Khristu, ndipo ndi wodzazidwa ndi Khristuyo amene amadzaza zinthu zonse kotheratu. Kale inu munali akufa chifukwa cha zolakwa zanu ndi machimo anu. Pa nthaŵi imeneyo, munkayenda m'zoipa potsata nzeru zapansipano, ndipo munkamvera mkulu wa aulamuliro amumlengalenga. Mkuluyo ndi mzimu woipa umene ukugwira ntchito tsopano pakati pa anthu oukira Mulungu. Nthaŵi imene ija ifenso tonse tinali ndi moyo wonga wao, ndipo tinkatsata zilakolako za khalidwe lathu lokonda zoipa. Tinkachitanso zilizonse zimene matupi athu ndi maganizo athu ankasirira. Nchifukwa chake, mwachibadwa chathu, tinali oyenera mkwiyo wa Mulungu, monga anthu ena onse. Koma Mulungu ndi wachifundo chachikulukulu, adatikonda ndi chikondi chachikulu kopambana. Motero, pamene tinali akufa chifukwa cha machimo athu, Iye adatipatsa moyo pamodzi ndi Khristu. Kukoma mtima kwa Mulungu ndi kumene kudakupulumutsani. Popeza kuti tili mwa Khristu Yesu, Mulungu adachita ngati kutiwukitsa kwa akufa pamodzi naye, kuti choncho atipatse malo aulemu pamodzi naye m'dziko la Kumwamba. Adachita zimenezi kuti mwa chifundo chake chimene adatichitira mwa Khristu Yesu, aonetse kwa nthaŵi zonse zam'tsogolo kuti ngwokomadi mtima kopambana. Ndi kukoma mtima kwa Mulungu kumene kudakupulumutsani pakukhulupirira. Simudapulumuke chifukwa cha zimene inuyo mudaachita ai, kupulumuka kwanu ndi mphatso ya Mulungu. Munthu sapulumuka chifukwa cha ntchito zake, kuwopa kuti angamanyade. Mulungu ndiye adatipanga. Adatilenga mwa Khristu Yesu kuti moyo wathu ukhale wogwira ntchito zabwino zimene Iye adakonzeratu kuti tizichite. Inu amene mtundu wanu sindinu Ayuda, kumbukirani m'mene munaliri kale. Ayuda amadzitchula oumbala, chifukwa cha mwambo umene amachita pa thupi lao, ndipo inu amakutchulani osaumbala. Tsono kumbukirani kuti nthaŵi imene ija munali opanda Khristu. Munali alendo, ndipo simunali a mtundu wa anthu osankhidwa ndi Mulungu. Munali opanda gawo pa zimene Mulungu, mwa zipangano zake, adaalonjeza anthu ake. Munkakhala pansi pano opanda chiyembekezo, opandanso Mulungu. Koma tsopano, mwa Khristu Yesu, inu amene kale lija munali kutali ndi Mulungu, mwakhala pafupi, chifukwa cha imfa ya Khristu. Khristu mwini wake ndiye mtendere wathu. Iye adasandutsa Ayuda ndi anthu a mitundu ina kuti akhale amodzi. Pakupereka thupi lake, adagamula khoma la chidani limene linkatilekanitsa. Iye adathetsa Malamulo a Mose pamodzi ndi malangizo ake ndi miyambo yake. Adachita zimenezi kuti kuchokera ku mitundu iŵiri ija, alenge mtundu umodzi watsopano, wokhala mwa Iye, kuti choncho adzetse mtendere. Khristu adafa pa mtanda kuti athetse chidani, ndipo kuti mwa mtandawo aphatikize pamodzi m'thupi limodzi mitundu iŵiriyo, ndi kuiyanjanitsa ndi Mulungu. Khristu adadzalalika Uthenga Wabwino wa mtendere kwa inu a mitundu inanu, amene munali kutali ndi Mulungu, ndiponso kwa Ayuda, amene anali pafupi naye. Tsopano kudzera mwa Khristu ife tonse, Ayuda ndi a mitundu ina, tingathe kufika kwa Atate mwa Mzimu Woyera mmodzi yemweyo. Nchifukwa chake tsono, inu amene simuli Ayuda, sindinunso alendo kapena akudza ai, koma ndinu nzika pamodzi ndi anthu ake a Mulungu, ndiponso ndinu a m'banja lake la Mulungu. Ndinu omangidwa pamodzi m'nyumba yomangidwa pa maziko amene ndi atumwi ndi aneneri, ndipo Khristu Yesu mwini ndiye mwala wapangodya. Mwa Iyeyu nyumba yonse ikumangidwa molimba, ndipo ikukula kuti ikhale nyumba yopatulika ya Ambuye. Mwa Iyeyu inunso mukumangidwa pamodzi ndi ena onse, kuti mukhale nyumba yokhalamo Mulungu mwa Mzimu Woyera. Nchifukwa chake ine Paulo ndimakupemphererani. Ndine womangidwa m'ndende chifukwa chotumikira Khristu ndi kugwirira ntchito inu amene simuli Ayuda. Kumva mudamva za ntchito imene mwa ufulu wake Mulungu adandipatsa, yolalika pakati panu za kukoma mtima kwake. Adandiwululira chinsinsi chake, monga ndidakulemberani mwachidule posachedwapa. Pamene muŵerenga zimenezi, mungathe kuwona kuti ndikumvetsetsadi chinsinsi chonena za Khristu. Chinsinsi chimenechi anthu a mibadwo yakale sadachidziŵe, koma Mulungu wachiwulula tsopano mwa Mzimu Woyera kwa atumwi ake oyera mtima, ndiponso kwa aneneri ake. Chinsinsicho nchakuti mwa Uthenga Wabwino anthu a mitundu ina nawonso ngoyenera kulandira madalitso a Mulungu pamodzi ndi Ayuda. Pamodzinso ndi Ayuda ali ziwalo za thupi limodzi, ndipo mwa Khristu Yesu amalandira nao lonjezo la Mulungu. Mwa kukoma mtima kwake Mulungu adandisandutsa wolalika Uthenga Wabwino umenewu, ndipo pakutero adaonetsapo mphamvu yake. Pakati pa anthu onse a Mulungu ine ndine wamng'ono koposa, komabe Mulungu adandipatsa ineyo ntchito iyi, yakuti ndilalikire anthu a mitundu ina za chuma chopanda malire, chimene Mulungu amatipatsa mwa Khristu. Adandipatsanso ntchito yofotokozera anthu onse za m'mene Mulungu adzachitira zonse zimene Iye adakonzeratu mwa chinsinsi chake. Mulungu amene adalenga zonse, adasunga chinsinsichi chikhalire, nthaŵi isanayambe. Tsopano afuna kuti kudzera mwa Mpingo, mafumu ndi aulamuliro onse a Kumwamba adziŵe nzeru za Mulungu zamitundumitundu. Mulungu adachita zimenezi kuti zichitikedi zimene Iye adakonzeratu mwa Khristu Yesu Ambuye athu chikhalire, nthaŵi isanayambe. Popeza kuti timakhulupirira Iyeyu, tingathe kulimba mtima kuyandikira kwa Mulungu mosakayika konse. Ndikukupemphani tsono kuti musataye mtima chifukwa chakuti ndikukusaukirani. Kwenikweni muyenera kunyadira chifukwa cha kusauka kwangaku. Nchifukwa chake tsono ndikugwadira Atate, amene banja lililonse Kumwamba ndi pansi pano limatchulidwa ndi dzina lao. Ndikupempha Mulungu kuti kuchokera m'chuma cha ulemerero wake akupatseni mphamvu, ndipo mwa Mzimu wake Woyera alimbitse moyo wanu wauzimu. Ndikupemphera kuti mwa chikhulupiriro chanu Khristu akhazikike m'mitima mwanu, kuti muzike mizu yanu m'chikondi, ndiponso kuti mumange moyo wanu wonse pa chikondi. Ndikupempha Mulungu kuti, pamodzi ndi anthu ake onse, muthe kuzindikira kupingasa kwake ndi kutalika kwake, kukwera kwake ndi kuzama kwake kwa chikondi cha Khristu. Ndithu ndikupemphera kuti mudziŵe chikondi chija cha Khristu chopitirira nzeru za anthu, kuti mudzazidwe kotheratu ndi moyo wa Mulungu mwini. Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza. Mulungu alandire ulemuwo mu Mpingo ndi mwa Khristu Yesu pa mibadwo yonse mpaka muyaya. Amen. Nchifukwa chake ine, womangidwa m'ndende chifukwa chotumikira Ambuye, ndikukupemphani kuti, chifukwa Mulungu adakuitanani, muziyenda moyenerana ndi kuitanidwako. Muzikhala odzichepetsa, ofatsa ndi opirira nthaŵi zonse. Muzilezerana mtima mwachikondi, ndipo muziyesetsa kusunga umodzi mwa Mzimu Woyera pa kulunzana mu mtendere. Pali thupi limodzi ndiponso Mzimu Woyera mmodzi, monganso pali chiyembekezo chimodzi chimene Mulungu adakuitanirani. Pali Mbuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi. Pali Mulungu mmodzi amene ali Atate a anthu onse. Iye ali pamwamba pa onse, amagwira ntchito kudzera mwa onse, ndipo ali mwa onse. Komabe aliyense wa ife adalandira mphatso yakeyake yaulere, molingana ndi m'mene Khristu amaperekera mphatso zake. Paja mau a Mulungu akuti, “Pamene adakwera Kumwamba, adatenga chigulu cha am'ndende, ndipo adagaŵira anthu mphatso.” Tsono mau akuti “adakwera” tanthauzo lake nchiyani? Ndiye kuti poyamba adaatsikira pansi penipeni pa dziko. Iye amene adaatsika, ndi yemweyo amene adakwera, nabzola Kumwamba konse, kuti zinthu zonse zikhale zodzaza ndi Iye. Iyeyu ndiye amene “adapereka mphatso kwa anthu.” Mphatso zake zinali zakuti ena akhale atumwi, ena aneneri, ena alaliki, ena abusa ndi aphunzitsi. Ntchito yao inali yakuti akonzeretu anthu a Mulungu kuti akagwire ntchito yotumikira, ndi kulimbitsa Mpingo umene uli thupi la Khristu. Motero potsiriza, tonse tidzafika ku umodzi umene umapezeka pakukhulupirira, ndiponso pakudziŵa Mwana wa Mulungu. Pamenepo tidzakhwima ndithu, ndi kufika pa msinkhu wathunthu wa Khristu. Sitidzakhalanso ngati ana akhanda ogwedezekagwedezeka ndi mafunde, ndiponso otengekatengeka ndi mphepo iliyonse ya zophunzitsa za anthu onyenga amene amasokeretsa anthu ndi kuchenjera kwao Kwenikwenitu pakulankhula zoona ndi mtima wachikondi, tizikula pa zonse mwa Khristu. Iye ndiye mutu, umene umalamula thupi lonse, ndi kulilumikiza pamodzi ndi mfundo zake zonse. Motero chiwalo chilichonse chimagwira ntchito yake moyenera, ndipo thupi lonse limakula ndi kudzilimbitsa ndi chikondi. Tsono m'dzina la Ambuye ndikukuuzani, ndipo ndikunenetsa, kuti musayendenso monga amachitira akunja potsata maganizo ao achabe. Nzeru zao zidachita chidima, sangalandire nao konse moyo wa Mulungu chifukwa cha umbuli umene udadza mwa iwo kaamba ka kuuma mtima kwao. Mitima yao idaludzulala ndipo adangodzipereka ku zonyansa, kuti azichita zoipa zilizonse mosadziletsa. Koma umu si m'mene inu mudaphunzirira za Khristu ai, ngatitu mudamva za Iyeyo, ngatinso mudaphunzitsidwa za Iye, motsata choona chimene chili mwa Yesu. Mudaphunzira kuti muleke mayendedwe anu akale, muvule moyo wanu wakale uja umene unkadziwononga ndi zilakolako zake zonyenga. Mtima wanu, umene uli gwero la maganizo anu, usanduke watsopano. Ndipo muvale moyo watsopano, umene Mulungu adaulenga, wofanafana naye. Apo mudzakhala olungama ndi oyera mtima kwenikweni. Tsono lekani kunama. Aliyense azilankhula zoona zokhazokha ndi mkhristu mnzake, pakuti tonse pamodzi mogwirizana ndife ziwalo za thupi la Khristu. Inde mwina nkupsa mtima, koma musachimwe, ndipo musalole kuti dzuŵa likuloŵereni muli chikwiyire. Musampatse mpata Satana woti akugwetseni. Amene ankaba, asabenso, koma makamaka azigwira ntchito kolimba ndi kumachita zolungama ndi manja ake, kuti akhale nkanthu kopatsa osoŵa. M'kamwa mwanu musatuluke mau aliwonse oipa, koma muzinena mau okhaokha abwino ndi olimbitsa mtima monga kungafunikire, kuti mupindulitse anzanu omva mau anuwo. Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera amene Mulungu adakusindikizani chizindikiro chake chotsimikizira kuti ndinu ake pa tsiku limene Mulunguyo adzatipulumutse kwathunthu. Muchotseretu pakati panu kuzondana, kukalipa, ndiponso kupsa mtima. Musachitenso chiwawa, kapena kulankhula mau achipongwe, tayani kuipa konse. Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso. Tsono popeza kuti ndinu ana okondedwa a Mulungu, muziyesa kumtsanzira. Muzikondana, monga Khristu adatikonda ife, nadzipereka kwa Mulungu chifukwa cha ife. Adadzipereka ngati chopereka ndi nsembe ya fungo lokondweretsa Mulungu. Popeza kuti ndinu anthu a Mulungu, ndiye kuti dama kapena zonyansa, kapena masiriro oipa zisatchulidwe nkomwe pakati panu. Ndiponso musamalankhule zolaula, zopusa, kapena zopandapake, koma muzilankhula zoyamika Mulungu. Mudziŵe ichi, kuti munthu aliyense wadama, kapena wochita zonyansa, kapena wa masiriro oipa (pakuti wa masiriro oipa ali ngati wopembedza fano) sadzaloŵa nao mu Ufumu wa Khristu ndi wa Mulungu. Munthu wina aliyense asakupusitseni ndi mau onyenga, pakuti zinthu zotere ndizo zimadzetsa ukali wa Mulungu pa anthu omupandukira. Nchifukwa chake musamagwirizane nawo anthu otere. Inunso kale mudaali mu mdima, koma tsopano muli m'kuŵala, popeza kuti ndinu ao a Ambuye. Tsono muziyenda ngati anthu okhala m'kuŵala. Pajatu pamene pali kuŵala, pamapezekanso ubwino wonse, chilungamo chonse ndi choona chonse. Muziyesa kudziŵa kwenikweni zimene zingakondweretse Ambuye. Musayanjane nawo anthu ochita zopanda pake za mdima, koma muŵatsutse. Paja zimene iwo amachita mobisa, ngakhale kuzitchula komwe kumachititsa manyazi. Koma kuŵala kumaunika zinthu, ndipo zonse zimaonekera poyera. Motero chilichonse choonekera poyera, chimasanduka kuŵala. Nchifukwa chake amati, “Dzuka wam'tulo iwe, uka kwa akufa, ndipo Khristu adzakuŵalira.” Samalirani bwino mayendedwe anu. Musayende monga anthu opanda nzeru, koma monga anthu anzeru. Mukhale achangu, osataya nthaŵi yanu pachabe, pakuti masiku ano ngoipa. Nchifukwa chake musakhale opusa, koma dziŵani zimene Ambuye afuna kuti muchite. Musaledzere vinyo, kumeneko nkudzitaya, koma mudzazidwe ndi Mzimu Woyera. Muzichezerana ndi mau a masalimo ndi a nyimbo za Mulungu ndi zauzimu. Ndipo muziimbira Ambuye mopolokezana ndi mtima wanu wonse. Muziyamika Mulungu Atate nthaŵi zonse chifukwa cha zonse, m'dzina la Ambuye athu Yesu Khristu. Inu amene mumaopa Khristu, muzimverana. Inu akazi, muzimvera amuna anu, monga mumamvera Ambuye. Paja mwamuna ndi mutu wa mkazi wake, monga momwe Khristu ali mutu wa Mpingo, umene uli thupi lake, ndipo Iye mwini ndi Mpulumutsi wa Mpingowo. Tsono monga Mpingo umamvera Khristu, momwemonso akazi azimvera amuna ao pa zonse. Inu amuna, muzikonda akazi anu, monga momwe Khristu adakondera Mpingo, nadzipereka chifukwa cha Mpingowo. Adachita zimenezi kuti aupatule ukhale wakewake, atauyeretsa pakuutsuka ndi madzi ndiponso ndi mau ake. Adafuna kuti akauimike pamaso pake uli waulemerero, wopanda banga kapena makwinya, kapena kanthu kena kalikonse kouipitsa, koma uli woyera ndi wangwiro kotheratu. Momwemonso amuna azikonda akazi ao, monga momwe eniakewo amakondera matupi ao. Amene amakonda mkazi wake, ndiye kuti amadzikonda iye yemwe. Palibiretu munthu amene amadana ndi thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulisamala bwino, monga momwe Khristu amachitira Mpingo wake. Amatero chifukwa Mpingowo ndi thupi lake, ndipo ife ndife ziwalo zake. Paja mau a Mulungu akuti, “Nchifukwa chake mwamuna adzasiye atate ndi amai ake, nkukaphatikizana ndi mkazi wake, kuti aŵiriwo asanduke thupi limodzi.” Mau ameneŵa akutiwululira chinsinsi chozama, ndipo ndikuti chinsinsicho nchokhudza Khristu ndi Mpingo. Komabe akunenanso za inu, kuti mwamuna aliyense azikonda mkazi wake monga momwe amadzikondera iye mwini, ndiponso kuti mkazi aliyense azilemekeza mwamuna wake. Inu ana, popeza kuti ndinu ake a Khristu, muzimvera anakubala anu, pakuti zimenezi ndiye zoyenera. Mau a Mulungu akuti, “Lemekeza atate ako ndi amai ako.” Limeneli ndiye lamulo loyamba kukhala ndi lonjezo. Lonjezolo likuti, “Ukatero, udzakhala wodala, ndipo moyo wako udzakhala wautali pansi pano.” Inu atate, musamaŵapsetsa mtima ana anu, koma muziŵalera bwino pakuŵasungitsa mwambo ndi malangizo a Ambuye. Inu akapolo, ambuye anu a pansi pano muziŵamvera mwamantha ndi monjenjemerera. Muzichita zimenezi ndi mtima woona, ngati kuti mukuchitira Khristu yemwe. Musazichite mwachiphamaso chabe, ngati kuti mukungofuna kukondweretsa anthu. Koma ngati akapolo a Khristu, muzichita ndi mtima wonse zimene Mulungu afuna. Muzitumikira mosangalala, ngati kuti mukutumikira Ambuye, osati anthu chabe. Mukudziŵa kuti Ambuye adzampatsa munthu aliyense mphotho chifukwa cha ntchito yake yabwino imene adaigwira, ngakhale munthuyo ndi kapolo kapena mfulu. Inu ambuye, muziŵachitiranso chimodzimodzi akapolo anu, ndipo muleke zoŵaopseza. Paja mukudziŵa kuti iwoŵa ndi inuyo, nonse muli ndi Mbuye wanu Kumwamba, ndipo Iyeyo alibe tsankho. Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu. Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana. Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga. Nchifukwa chake valani zida zonse za Mulungu. Pamenepo mudzatha kulimbika, osagonja pa tsiku loipa, ndipo mutatsiriza kulimbanaku, mudzaimabe kuti nji. Imirirani tsono mutavala choona ngati lamba m'chiwuno mwanu. Valani chilungamo ngati chovala chachitsulo chotchinjirizira pachifuwa panu. Ndipo changu chanu polalika Uthenga Wabwino wa mtendere chikhale ngati nsapato zanu. Nthaŵi zonse mukhale ndi chikhulupiriro ngati chishango chanu chokutetezani, chimene mudzatha kuzimitsira mivi yonse yoyakamoto ya Satana. Landirani chipulumutso ngati chisoti chanu, ndi mau a Mulungu ngati lupanga limene Mzimu Woyera akupatsani. Chitani zonse mopemphera, ndi kupempha chithandizo cha Mulungu nthaŵi zonse. Nthaŵi iliyonse muzipemphera motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Nchifukwa chake muchezere kupemphera mosalekeza, kupempherera anthu onse a Mulungu. Inenso muzindipempherera, kuti Mulungu aike mau m'kamwa mwanga pamene ndizilankhula, kuti ndidziŵitse anthu chinsinsi cha Uthenga Wabwino molimba mtima. Ngakhale ndili womangidwa m'ndende, ndine nthumwi ndithu chifukwa cha Uthenga Wabwinowu. Mundipempherere tsono kuti ndizilankhula molimba mtima za Uthenga Wabwinowu, monga ndiyenera kulankhulira. Tikiko adzakudziŵitsani zonse za ine ndi zimene ndikuchita. Iyeyu ndi mbale wathu wokondedwa, ndiponso mtumiki wokhulupirika pa ntchito ya Ambuye. Ndikumtuma kwa inu kuti mudziŵe za m'mene tiliri, ndipo kuti akulimbitseni mtima. Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu apatse abale onse mtendere, chikondi ndi chikhulupiriro. Onse okonda Ambuye athu Yesu Khristu ndi chikondi chosafa, Mulungu aŵadalitse. Ndife, Paulo ndi Timoteo, atumiki a Khristu Yesu. Tikulembera onse a mu mzinda wa Filipi, amene ali anthu ake a Mulungu mwa Khristu Yesu. Tikulemberanso oyang'anira Mpingo ndi atumiki ao. Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere. Ndimayamika Mulungu wanga nthaŵi zonse ndikamakukumbukirani. Nthaŵi zonse pamene ndikukupemphererani nonsenu, ndimapemphera mokondwa. Ndiyeneradi kuthokoza chifukwa mwakhala mukugwirizana nane ndi kundithandiza kufalitsa Uthenga Wabwino, kuchokera tsiku limene mudayamba kukhulupirira mpaka tsopano. Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu. Ndikuyeneradi kuganiza zotere za nonsenu, popeza kuti ndimakukondani kwambiri. Pakuti nonsenu ndinu ogwirizana nane ndithu, pamene ndili m'ndende ndiponso pamene ndikugwira ntchito iyi imene Mulungu adandipatsa mwa kukoma mtima kwake, ntchito ya kuteteza ndi kukhazikitsa Uthenga Wabwino. Mulungu akundichitira umboni kuti ndimakulakalakani kwambiri, pakuti ndimakukondani ndi mtima wonse, motsanzira chikondi cha Khristu Yesu mwini. Pemphero langa ndi lakuti chikondi chanu chinke chikukulirakulira pamodzi ndi nzeru ndi kumvetsetsa zinthu mozama. Pamenepo mudzadziŵa kusankha zimene zili zabwino kotheratu. Apo pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu mudzapezeka oyera mtima, ndi opanda cholakwa chilichonse. Ndipo moyo wanu udzakhala wodzaza ndi zipatso za chilungamo zimene mudzaonetsa mothandizidwa ndi Yesu Khristu, kuti anthu onse alemekeze ndi kutamanda Mulungu. Abale, ndikufuna kuti mudziŵe kuti zimene zandigwera, zathandiza ndithu kufalitsa Uthenga Wabwino. Mwakuti asilikali onse olonda nyumba ya mfumu, ndi ena onse kuno, adziŵa kuti ndili m'ndende chifukwa cha Khristu. Tsono chifukwa choti ndili m'ndende, abale ochuluka akulimba mtima mwa Ambuye, ndipo akulalika mau a Mulungu mopanda mantha. Alipodi ena amene amalalika Khristu chifukwa cha kaduka ndi kukonda mikangano. Koma aliponso ena amene amamlalika ndi mtima woona. Otsirizaŵa amamlalika chifukwa cha chikondi, popeza kuti amadziŵa kuti Mulungu adandikhazika muno kuti ndigwire ntchito yoteteza Uthenga Wabwino. Koma oyamba aja salalika Khristu moona. Amangodzikonda okha, ndipo amafuna kundiwonjezera zoŵaŵa pamene ndili m'ndende muno. Zili nkanthu ngati! Kaya amalalika mwachiphamaso, kaya moona, malinga nkuti Khristu akulalikidwa, pamenepo ine ndikukondwa. Ndipo sindidzaleka kukondwa podziŵa kuti chifukwa cha mapemphero anu ndiponso chithandizo cha Mzimu wopatsidwa ndi Yesu Khristu ndidzamasulidwa. Motero ndikuyembekeza ndi kukhulupirira ndi mtima wonse kuti sipadzakhala konse manyazi. Koma ndikuyembekeza kuti ndidzalimba mtima kulankhula poyera, kuti tsopanonso, monga nthaŵi zonse, Khristu alemekezedwe mwa ine, ngakhale ndikhale moyo, kapena ndimwalire. Kwa inetu moyo ndi Khristu amene, ndipo nayonso imfa ili ndi phindu. Koma ngati kukhalabe moyo kungandipatse mwai woti ndigwire ntchito yoonetsa zipatso, sindidziŵa kaya ndingasankhe chiti. Ndagwira njakata. Kwinaku ndikulakalaka kuti ndisiye moyo uno ndikakhale pamodzi ndi Khristu, pakuti chimenechi ndiye chondikomera koposa. Koma kwinakunso nkofunika kwambiri kuti ndikhale moyo chifukwa cha inuyo. Mosakayika konse ndikudziŵa kuti ndidzakhalapobe. Ndidzapitiriza kukhala nanu nonsenu, kuthandiza kuti chikhulupiriro chanu chizikula, ndipo chikupatseni chimwemwe koposa kale. Motero pamene ndidzafikanso kwanuko, mudzakhala ndi zifukwa zochuluka zonyadira Khristu Yesu chifukwa cha ine. Chachikulu nchakuti mayendedwe anu akhale oyenerana ndi Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Ngakhale ndibwere kudzakuwonani, kapena ndikhale kutali, ndikufuna kumva kuti mukulimbika ndi mtima umodzi. Ndikufunanso kumva kuti momvana ndi mothandizana mukumenya nkhondo chifukwa chokhulupirira Uthenga Wabwino, osalola kuti adani anu azikuwopsezani pa kanthu kalikonse. Zimenezi zidzaŵatsimikizira kuti iwowo adzaonongeka, koma inu mudzapulumuka. Mulungu ndiye amene adzakuchitirani zimenezi. Paja Iye adakupatsani mwai, osati wakungokhulupirira Khristu ai, komanso wakumva zoŵaŵa chifukwa cha Iye. Inunso mukumenya nkhondo yomwe ija imene mudandiwona ine ndikuimenya, yomwenso ndikumenyabe tsopano, monga mukumveramu. Mosapeneka, moyo wanu mwa Khristu umakulimbitsani mtima. Chikondi chake chimakuchotsani nkhaŵa. Mumakhala a mtima umodzi mwa Mzimu Woyera, ndipo mumamvera anzanu chifundo ndi chisoni. Nchifukwa chake ndikukupemphani kuti mundikondweretse kwenikweni pakuvomerezana maganizo ndi kukondana chimodzimodzi, kukhala a mtima umodzi ndi a cholinga chimodzi. Musamachita kanthu ndi mtima wodzikonda, kapena wodzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa, ndipo aliyense aziwona anzake kuti ngomuposa iyeyo. Musamangofuna zokomera inu nokha, koma zokomeranso anzanu. Motero nonse mukhale ndi mtima womwe uja umene adaali nawonso Khristu Yesu: Iyeyu anali ndi umulungu chikhalire, komabe sadayese kuti kulingana ndi Mulungu ndi chinthu choti achigwiritsitse. Koma adadzitsitsa kotheratu pakudzitengera umphaŵi wa kapolo, ndi kukhala munthu wonga anthu onse. Ali munthu choncho adadzichepetsa, adakhala womvera mpaka imfa, imfa yake yapamtanda. Chifukwa cha chimenechi Mulungu adamkweza kopambana, nampatsa dzina lopambana dzina lina lililonse. Adachita zimenezi kuti pakumva dzina la Yesu, zolengedwa zonse kumwamba, pansi pano ndi pansi pa dziko, zidzagwade pansi mopembedza, Zonse zidzavomereze poyera kuti, “Yesu Khristu ndi Ambuye,” ndipo pakutero zilemekeze Mulungu Atate. Nchifukwa chake, inu okondedwa anga, mwakhala omvera nthaŵi zonse pamene ndinali nanu. Nanji tsopano pamene sindili nanu, ndiye muzikhala omvera koposa. Mupitirize ndi kufikitsa chipulumutso chanu pa chimake mwamantha ndi monjenjemerera. Paja Mulungu ndiye amene amagwira ntchito mwa inu, muzifuna ndi kutha kuchita zimene zimkomera Iye. Muzichita zonse mosanyinyirika ndi mosatsutsapo, kuti mukhale angwiro ndi osalakwa, ana a Mulungu opanda chilema chilichonse pakati pa anthu onyenga ndi osokeretsa anzao. Pakati pa anthu otere mumaŵala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi, pakuŵauza mau opatsa moyo. Motero ine ndidzakhala ndi chifukwa chonyadira pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu. Pakuti pamenepo padzadziŵika kuti sindidathamange pachabe pa mpikisano wa liŵiro, ndipo khama langa pa ntchito silidapite pachabe. Ndipotu mwina mwake ndidzaphedwa, magazi anga nkukhala ngati otsiridwa pa nsembe imene chikhulupiriro chanu chikupereka kwa Mulungu. Ngati ndi choncho ndili wokondwa, ndipo ndikusangalala nanu pamodzi nonsenu. Chimodzimodzi inunso muzikondwa, ndi kusangalala nane pamodzi. Ngati Ambuye Yesu alola, ndikhulupirira kuti ndidzatha kutuma Timoteo kwanuko msanga, kuti mtima wanga ukhale pansi nditamva za kumeneko. Ndilibenso wina wonga amene ali ndi mtima wosamala za inu kwenikweni. Paja ena onse amangofuna zokomera iwo okha, osati zokomera Yesu Khristu. Koma mukudziŵa kuti mkhalidwe wa Timoteo ndi wotsimikizika kale kuti ngwabwino. Mukudziŵanso kuti adagwira mogwirizana nane ntchito yofalitsa Uthenga Wabwino, monga mwana ndi bambo wake. Ndikuyembekeza tsono kumtumiza kwa inu msanga, nditadziŵa za m'mene ziyendere zanga. Koma ndikhulupirira kuti, Ambuye akalola, inenso ndidzafika kwanuko msanga. Ndaganiza kuti nkofunikadi kuti ndikutumizireni mbale wathu uja, Epafrodito. Mudaamtuma kuti adzandithandize pa zosoŵa zanga, ndipo wagwiradi ntchito ndi kumenya nkhondo yachikhristu pamodzi ndi ine. Tsonotu akukulakalakani nonsenu, ndipo ndi wokhumudwa podziŵa kuti inu mudamva zoti iye ankadwala. Nzoonadi adaadwala zedi mpaka pafupi kufa. Mwai kuti Mulungu adamchitira chifundo. Ndipotu sadangochitira chifundo iye yekhayu, komanso ineyo, kuti chisoni changa chisakhale chosanjikizana. Nchifukwa chake ndikufunitsitsa ndithu kumtumiza kwa inu, kuti podzamuwonanso mudzasangalale, kutinso nkhaŵa yanga ichepeko. Mlandireni mwachikhristu ndi chimwemwe chachikulu. Anthu otere muziŵachitira ulemu. Chifukwa cha kugwira ntchito ya Khristu, iyeyu adaali pafupifupi kufa. Adaadzipereka osaopa ngakhale kutaya moyo wake kuti azindithandiza pa zimene inu simudathe kukwaniritsa pondithandiza. Abale anga, potsiriza ndikuti, “Muzikondwa mwa Ambuye.” Kukulemberaninso mau omwewo sikondilemetsa, ndipo mauwo ngokuthandizani kukhala osakayika. Chenjera nawoni ochita zaugalu aja, ndiye kuti ochita zoipa, anthu omangodula thupi chabe. Paja ifeyo ndiye oumbala enieni, ife amene timapembedza Mulungu motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Timanyadira Khristu Yesu, osadalira miyambo ya thupi chabe. Komabetu ineyo ndikadatha kudalira miyambo yathupiyi. Ngati alipo wina woganiza kuti ali ndi chifukwa chodalira miyambo yathupi yotere, ineyo ndili ndi chifukwa choposa apo. Pajatu ine ndidaumbalidwa pa tsiku lachisanu ndi chitatu nditabadwa. Ndine wa mtundu wa Israele, wa fuko la Benjamini, Mhebri weniweni wobadwa mwa makolo achihebri. Kunena za Malamulo achiyuda, ndinali wa gulu la Afarisi. Ndipo changu changa chinali chachikulu, kotero kuti ndinkazunza Mpingo. Kunena za chilungamo chopezeka pakutsata Malamulo, ineyo ndinali wopanda cholakwa. Koma chifukwa cha Khristu, zomwe kale ndinkaziyesa zaphindu, tsopano ndikuziwona kuti nzosapindula. Zoonadi, zonse ndikuziwona kuti nzosapindulitsa poziyerekeza ndi phindu lopambana la kudziŵa Khristu Yesu, amene ndi Ambuye anga. Chifukwa cha Khristuyo ndidalolera kutaya zonse, nkumaziyesa zinyalala, kuti potero phindu langa likhale Khristu, Iye ndi ine tikhale amodzi. Sindiyesanso pandekha kukhala wolungama pakutsata Malamulo, koma ndizikhala ndi chilungamo chopezeka pakukhulupirira Khristu, chilungamo chochokera kwa Mulungu, chochilandira pakukhulupirira. Chimene ndikufuna nchakuti ndidziŵe Khristu, ndiponso mphamvu zimene zidamuukitsa kwa akufa. Ndikufunanso kumva zoŵaŵa pamodzi naye ndi kufanafana naye pa imfa yake. Ndikuyesetsa kuchita zimenezi pokhulupirira kuti inenso ndidzakhala ndi moyo wosatha podzauka kwa akufa. Sindikunena kuti ndafikapo kale pa zimenezi, kapena kuti ndine wangwiro kale. Koma ndikuthamangabe ndi kuyesetsa kuzipata pakuti ndicho chinali cholinga cha Yesu Khristu pakundikopa kuti ndikhale wake. Abale, sindikuganiza konse kuti ndazipata kale. Koma pali chimodzi chokha chimene ndimachita: ndimaiŵala zakumbuyo, ndi kuyesetsa kufikira ku zakutsogolo. Ndikuthamangira ku mapeto a mpikisano wa liŵirowu, kuti ndikalandire mphotho Kumwamba, imene Mulungu akutiitanira kudzera mwa Khristu Yesu. Tsono ife tonse amene tili okhwima pa moyo wathu wauzimu, tikhale ndi mtima womwewo. Ngati pa zinthu zina muli ndi maganizo osiyana ndi ameneŵa, pameneponso Mulungu adzakuunikirani. Koma ngakhale zitani, tisatayepo kanthu pa zoona zimene takhala tikuzikhulupirira mpaka tsopano. Abale anga, nonse pamodzi muzinditsanzira ine, ndipo muziŵapenyetsetsa amene amayenda motsata chitsanzo chimene ife timakupatsani. Ndakhala ndikukuuzani kaŵirikaŵiri, ndipo tsopano ndikubwerezanso molira misozi, kuti pali ambiri amene mayendedwe ao akutsimikiza kuti amadana ndi mtanda wa Khristu. Mathero ao nkuwonongeka. Zosangalatsa thupi chabe ndizo zili ngati mulungu wao. Amanyadira zimene akadayenera kuchita nazo manyazi, ndipo amangoika mtima pa zapansipano zokha. Koma ife kwathu kwenikweni ndi Kumwamba, ndipo kumeneko kudzachokera Mpulumutsi amene tikumuyembekeza. Mpulumutsiyo ndi Ambuye Yesu Khristu. Iyeyo adzasandutsa matupi athu achabeŵa kuti akhale ofanafana ndi thupi lake laulemerero. Adzachita zimenezi ndi mphamvu zake zomwe zija zimene angathenso kugonjetsa nazo zinthu zonse. Tsono abale anga, ndimakukondani ndipo ndikukulakalakani. Mumandisangalatsa ndipo ndinu mphotho yanga imene ndimainyadira. Okondedwa anga, limbikani choncho mogwirizana ndi Ambuye. Yuwodiyayo ndi Sintikeyo ndaŵapemba, chonde akhale omvana, popeza kuti ndi abale mwa Ambuye. Ndiponso iwe, mnzanga weniweni pa ntchito yathuyi, bwanji uŵathandize azimaiŵa. Paja ameneŵa pofalitsa Uthenga Wabwino akhala akugwira ntchito kolimba pamodzi ndi ine ndi Klemensi ndi antchito anzanga ena onse, amene maina ao ngolembedwa m'buku la amoyo. Muzikondwa mwa Ambuye nthaŵi zonse. Ndikubwerezanso kuti, “Muzikondwa.” Kufatsa kwanu kuziwoneka pamaso pa anthu onse. Ambuyetu ali pafupi. Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika. Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu. Potsiriza, abale, muziika mtima pa zilizonse zabwino kwambiri ndi zotamandika, monga izi: zinthu zoona ndi zolemekezeka, zinthu zolungama, zoyera, zokongola, ndi zaulemu. Muzichita zimene mudaphunzira ndi kulandira kwa ine, ndiponso zimene mudamva kwa ine ndi kuwonera kwa ine. Pamenepo Mulungu amene amapatsa mtendere adzakhala nanu. Ndakondwa kwambiri mwa Ambuye kuti tsopano, patapita nthaŵi yaitali, mwayambanso kuwonetsa kuti mumandikumbukira. Kukumbukira munkandikumbukiradi, koma munkangosoŵa mpata woti muwonetsere. Sindikunena zimenezi modandaula kuti ndikusoŵa kanthu, pakuti ine ndaphunzira kukhutira ndi zimene ndili nazo. Kukhala wosauka ndimakudziŵa, kukhala wolemera ndimakudziŵanso. Pa zonse ndidaphunzira chinsinsi chake cha kukhala wokhutitsidwa, pamene ndapeza chakudya kapena ndili ndi njala, pamene ndili ndi zambiri kapena ndili wosoŵeratu. Ndingathe kuchita zonse chifukwa Khristu amandipatsa mphamvu. Komabe mudaachita bwino kundithandiza pa zovuta zanga. Inu Afilipi, mukudziŵa inu nomwe kuti pamene ndidachoka ku Masedoniya, masiku oyamba aja akulalika Uthenga Wabwino, panalibe mpingo wina wogwirizana nane pa zoyenera kulipira kapena kulandira, koma inu nokha. Pamene ndinali ku Tesalonika, mudatumiza kangapo zondithandiza pa zosoŵa zanga. Sikuti ndikuika mtima pa mphatso zanu ai, koma chimene ndikukhumba nchakuti pa zimene muli nazo, pawonjezedwe phindu. Ndalandiradi zonse, ndipo ndili nazo zochuluka. Ndili ndi zonse zofunika tsopano, popeza kuti ndalandira kwa Epafrodito zimene mudanditumizira. Zili ngati chopereka cha fungo lokoma, ngati nsembe imene Mulungu ailandira ndi kukondwera nayo. Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa. Mulungu Atate athu alemekezedwe mpaka muyaya. Amen. M'dzina la Khristu Yesu mundiperekereko moni kwa aliyense wamumpingo. Akukupatsani moni abale amene ndili nawo pamodzi kuno. Akukupatsani moni anthu onse a Mulungu amene ali kuno, makamakanso ogwira ntchito ku nyumba ya Mfumu ya ku Roma. Ambuye Yesu Khristu akudalitseni. Ndine, Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa kufuna kwa Mulungu. Ndili limodzi ndi Timoteo, mbale wathu. Tikulembera inu osankhidwa ndi Mulungu okhala ku Kolose, abale athu okhulupirika mwa Khristu. Mulungu Atate athu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere. Tikamakupemphererani, nthaŵi zonse timathokoza Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Timathokoza chifukwa tamva kuti mumakhulupirira Khristu Yesu, ndiponso kuti mumakonda anthu onse a Mulungu. Gwero la zonsezi ndi chiyembekezo chimene muli nacho chodzalandira zimene Mulungu akukusungirani Kumwamba. Mudamva za zimenezi pamene mau oona, adakufikani poyamba paja. Mau oonawo ndi Uthenga Wabwino. Uthenga Wabwinowu ukubala zipatso ndi kufalikira pa dziko lonse lapansi, monga momwe wachitiranso pakati panu, kuyambira tsiku limene mudamva ndi kumvetsa za kukoma mtima kwa Mulungu. Mudaphunzira zimenezi kwa Epafra, mtumiki mnzathu wokondedwa. Iye uja akugwirira ntchito Khristu mokhulupirika m'malo mwathu. Ndiye amene adatidziŵitsa za chikondi chomwe Mzimu Woyera adaika mwa inu. Nchifukwa chake, kuyambira tsiku limene tidamva zimenezi, sitileka kukupemphererani. Timapempha Mulungu kuti akudzazeni ndi nzeru ndi luntha, zimene Mzimu Woyera amapatsa, kuti mumvetse zonse zimene Iye afuna. Pamenepo mudzatha kuyenda m'njira zimene Ambuye amafuna, ndi kuŵakondweretsa pa zonse. Pakugwira ntchito zabwino zamitundumitundu, moyo wanu udzaonetsa zipatso, ndipo mudzanka muwonjezerawonjezera nzeru zanu za kudziŵa Mulungu. Timapempheranso kuti Mulungu akulimbikitseni ndi mphamvu yake yaulemerero, kuti muzipirira zonse ndi mitima yoleza ndi yosangalala. Ndipo timapemphera kuti muziyamika Atate, amene adakuyenerezani kuti mudzalandire nao madalitso onse amene amasungira anthu ao mu ufumu wa kuŵala. Adatilanditsa ku mphamvu za mdima wa zoipa, nkutiloŵetsa mu Ufumu wa Mwana wake wokondedwa. Mwa Iyeyu Mulungu adatiwombola, ndiye kuti adatikhululukira machimo athu. Khristuyo ndiye chithunzi chenicheni cha Mulungu wosaoneka. Iye ndiye Mwana wake woyamba, wolamulira zolengedwa zonse. Kudzera mwa Iye Mulungu adalenga zonse zakumwamba ndi zapansipano, zooneka ndi zosaoneka, mafumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu ena onse. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, zonsezo adalengera Iyeyo. Iyeyo analipo zinthu zonse pakadalibe, mwa Iye zinthu zonse zimalunzana pamodzi. Iye ndiyenso mutu wa mpingo thupi lake. Ndiye chiyambi chake, Woyambirira mwa ouka kwa akufa, kuti pa zonse Iye akhale wopambana ndithu. Kudakomera Mulungu kuti umulungu wake wonse ukhalemo mwa Khristuyo. Mwa Iyeyo Mulungu adafuna kuyanjanitsanso zinthu zonse ndi Iye mwini, zapansipano ndi za Kumwamba. Adachita zimenezi pakudzetsa mtendere kudzera mwa imfa ya Mwana wake pa mtanda. Kale inu munali kutali ndi Mulungu, ndipo munkadana naye m'maganizo anu ndi m'ntchito zanu zoipa. Koma tsopano, kudzera mwa imfa ya Mwana wake m'thupi lake, Mulungu wakuyanjanitsaninso ndi Iye mwini. Adachita zimenezi kuti pamaso pake muthe kuwoneka muli oyera mtima, opanda banga kapena cholakwa chilichonse. Koma tsono muzikhala okhazikika kolimba pa maziko a chikhulupiriro chanu, osasunthika pa chiyembekezo chofumira ku Uthenga Wabwino umene mudamva. Uthenga Wabwinowu walalikidwa kwa anthu a pa dziko lonse lapansi, ndipo Mulungu ndiye adandipatsa ine, Paulo, ntchito yoti ndiwulalike. Tsopano ndakondwa kuti ndikukuvutikirani. Pakuti pakumva zoŵaŵazo, ndikutsiriza m'thupi mwanga zotsala za masautso a Khristu kuthandiza thupi lake, ndiye kuti Mpingo. Ndipo ine ndine mtumiki wa Mpingowu, pakuti Mulungu ndiye adandipatsa ntchitoyi yoti ndikulalikireni kwathunthu mau ake. Mauwo ndi chinsinsi chozama chimene chinali chobisika chikhalire kwa mibadwo yonse, koma tsopano Mulungu wachiwululira anthu ake. Cholinga cha Mulungu ndi cha kudziŵitsa anthuwo kukoma kwake kwa chinsinsicho ndi ulemerero wake pakati pa anthu akunja. Chinsinsicho nchakuti Khristu ali mwa inu, ndipo Iye amakupatsani chiyembekezo cha kudzalandira ulemerero. Khristuyo ndiye amene timamlalika. Timachenjeza ndi kuphunzitsa munthu aliyense ndi nzeru zonse zimene tili nazo. Pakuti tikufuna kusandutsa munthu aliyense kuti akhale wangwiro mwa Khristu. Ndi cholinga chimenechi ndikugwiradi ntchito kwambiri ndi mphamvu ya Khristu imene ikugwira ntchito kolimba mwa ine. Ndikufuna kuti mudziŵe kuti ndikukuvutikirani kwambiri, inuyo ndi anzanu a ku Laodikea, ndi ena onse amene sitidaonane nawo maso ndi maso chikhalire. Ndikufuna kuti zimenezi ziŵalimbitse mtima, ndipo azilunzana pamodzi m'chikondi, azikhala odzaza ndi nzeru zomvetsa zinthu. Motero adzatha kudziŵa mozama chinsinsi cha Mulungu chonena za Khristu. Mwa Iyeyu mudzapeza chuma chonse chobisika, ndiye kuti nzeru ndi luntha. Ndikunenatu zimenezi, kuwopa kuti wina aliyense angakukopeni ndi mau onyenga. Pakuti ngakhale sindili nanu m'thupi, komabe mumtimamu ndili nanu pamodzi. Ndipo ndakondwa kuwona kuti mukulongosola bwino zonse, ndi kuti chikhulupiriro chanu mwa Khristu nchosagwedezeka konse. Tsono popeza kuti mudavomereza kuti Khristu Yesu ndi Mbuye wanu, moyo wanu wonse ukhale wolunzana naye. Mukhale ozika mizu mwa Iye. Mupitirire kumanga moyo wanu pa Iye. Mulimbike kukhulupirira monga momwe mudaphunzirira, ndipo muzikhala oyamika kwambiri. Chenjerani kuti wina aliyense angakusokonezeni ndi mau olongosola nzeru zapatali. Ameneŵa ndi mau onyenga chabe. Paja nzeru zimenezi zimangochokera ku miyambo ya anthu, ndi ku maganizo ao okhudza zapansipano, osati kwa Khristu ai. Pakuti m'thupi la Khristu umulungu wonse umakhalamo wathunthu. Ndipo mwa Iye inu mudapatsidwa moyo wonse wathunthu. Iye ndiye mutu wolamulira maulamuliro onse ndi mphamvu zonse zosaoneka. Mwa Iye mudachita ngati kuumbalidwa, osatitu kuumbala kwa anthuku ai, koma kuvula khalidwe lanu lokonda zoipa; kuumbala kumene amachita Khristu nkumeneku. Pamene mudabatizidwa, mudachita ngati kuikidwa m'manda pamodzi ndi Khristu. Ndipo ndi ubatizowo mudaukitsidwanso pamodzi naye, pakukhulupirira mphamvu za Mulungu amene adamuukitsa kwa akufa. Inu kale munali akufa chifukwa cha machimo anu, ndiponso chifukwa munali osaumbalidwa mu mtima. Koma tsopano Mulungu wakupatsani moyo pamodzi ndi Khristu. Adatikhululukira machimo athu zonse. Adafafaniza kalata ya ngongole yathu, yonena za Malamulo a Mose. Kalatayo inali yotizenga mlandu, koma Iye adaichotsa pakuikhomera pa mtanda. Motero mwa Khristu Mulungu adaŵalanda zida maufumu ndi maulamuliro onse, ndipo pamaso pa onse, adaŵayendetsa ngati akaidi pa mdipiti wokondwerera kupambana kwake. Wina aliyense asakuzengeni mlandu pa nkhani yokhudza zakudya kapena zakumwa, kapena pa zokhudza masiku a chikondwerero, kapena a mwezi wokhala chatsopano, kapena pa zokhudza tsiku la Sabata. Zonsezi ndi chithunzithunzi chabe cha zinthu zenizeni zimene zilikudza, koma zenizenizo ndi Khristu amene. Wina aliyense asakuletseni kupata mphothoyo. Iwo aja amakonda kudziwonetsa ngati odzichepetsa, popembedza amatamanda angelo. Amaika mtima pa zimene akuti adaziwona m'masomphenya. Amadzitukumula popanda chifukwa, popeza kuti amangotsata nzeru za anthu, osakangamira Khristu amene ali mutu wa Mpingo. Komatu mwa Khristu thupi lonse limalandira mphamvu, ndi kulumikizika pamodzi mwa mfundo zake ndi mitsempha yake. Motero thupi limakula monga momwe Mulungu afuna kuti likulire. Mudafa pamodzi ndi Khristu, ndiye kuti simulamulidwanso ndi miyambo ya dziko lapansi. Tsono bwanji mukuchita ngati kuti moyo wanu ukudalirabe zapansipano? Bwanji mukuŵamvera malamulo onga aŵa akuti, “Usagwire chakuti”, “Usakhudze chakuti”? Malamulo ameneŵa ndi zophunzitsa zimenezi ndi za anthu chabe, ndipo zimangokhudza zinthu zimene zimatha, anthu akamazigwiritsa ntchito. Kwinaku mauwo amaoneka ngati anzeru, pakuti amalamula anthu zambiri pa za kupembedza, za kudzichepetsa ndi za kuzunza thupi lao. Komabe malamulowo alibe phindu, ndipo sathandiza konse kugonjetsa khalidwe longosangalatsa thupi. Tsono ngati mudaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mtima pa zinthu za Kumwamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu. Muzifunafuna za Kumwamba, osati zapansipano. Pakuti kunena za moyo wakalewo mudafa, ndipo moyo wanu watsopano ndi wobisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu. Khristu ndiye moyo wanu weniweni tsopano, choncho pamene Iye adzaonekerenso, inunso mudzaonekera mu ulemerero pamodzi naye. Iphani tsono zilakolako za mu mtima wanu woumirira zapansipano, monga dama, zonyansa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoipa, ndiponso kusirira zinthu mwaumbombo. Kusirira kotereku sikusiyana ndi kupembedza mafano. Chifukwa cha zinthu zotere Mulungu amaŵakwiyira anthu osamumvera. Inunso kale makhalidwe anu anali omwewo, munkachita zomwezo. Koma tsopano musachitenso zonsezi, monga kukalipa, kukwiya, kuipa mtima, ndi mijedu. Pakamwa panu pasamatulukenso mau otukwana kapena onyansa. Musamauzana mabodza, pakuti mwachita ngati mwavula moyo wanu wakale, pamodzi ndi zochitachita zake zoipa, ndipo mwavala moyo watsopano. Moyo umenewu, Mlengi wanu akuukonzabe kosalekeza, kuti mudzamdziŵe kwenikweni ndi kufanafana naye. M'moyo watsopanowu palibenso zoti uyu ndi Myuda kapena wosakhala Myuda, woumbala kapena wosaumbala, munthu wachilendo, munthu wosaphunzira, kapolo kapena mfulu, koma Khristu basi ndiye wopambana onse, ndipo amakhala mwa onse. Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira. Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana. Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu. Mtendere wa Khristu uzikutsogolerani m'mitima mwanu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale nawo mtendere umenewu, popeza kuti ndinu ziwalo za thupi limodzi. Muzikhala oyamika. Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu. Chilichonse chimene mungachite, kaya nkulankhula, kaya nkugwira ntchito, muchichite m'dzina la Ambuye Yesu ndi kuthokoza Mulungu Atate kudzera mwa Iye. Inu akazi, muzimvera amuna anu, monga ayenera kuchitira okhala mwa Ambuye. Inu amuna, muzikonda akazi anu, musamaŵavutitse ai. Inu ana, muzimvera anakubala anu pa zonse, pakuti kutero kumakondwetsa Ambuye. Inu atate, musamaŵapsetsa mtima ana anu, kuti angataye mtima. Inu antchito, muziŵamvera pa zonse ambuye anu apansipano. Musamangochitatu zimenezi pamene muli pamaso pao kuti akuyamikireni, koma muziŵamvera ndi mtima wonse, chifukwa choopa Ambuye. Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai. Paja mukudziŵa kuti Ambuye adzakupatsani mphotho. Mphothoyo ndi madalitso amene adalonjeza kudzapatsa anthu ake. Ambuye amene mukuŵatumikirawo ndi Khristu. Koma munthu amene amachita zosalungama, zidzamubwerera, chifukwa Mulungu amaweruza mosakondera. Inu ambuye, antchito anu muzikhalitsana nawo mwachilungamo ndi moyenera, podziŵa kuti inunso muli ndi Mbuye wanu Kumwamba. Muzipemphera mosafookera, ndipo pamene mukupemphera, muzikhala tcheru ndiponso oyamika Mulungu. Ifeyonso muzitipempherera kuti Mulungu atipatse mwai woti tilalike mau ake, makamaka kuti tilengeze chinsinsi chozama chokhudza Khristu. Chifukwa cha kulalika chinsinsichi ndine womangidwa m'ndende muno. Mundipempherere tsono kuti ndichifotokoze bwino monga ndiyenera. Mayendedwe anu pakati pa anthu akunja azikhala anzeru, ndipo muzichita changu, osataya nthaŵi pachabe. Nthaŵi zonse mau anu akhale okoma, opindulitsa ena, kuti potero mudziŵe m'mene muyenera kuyankhira munthu aliyense. Tikiko, mbale wathu wokondedwa, adzakudziŵitsani zonse za ine. Iyeyo ndi mtumiki wokhulupirika, wantchito mnzathu pa ntchito ya Ambuye. Nchifukwa chake ndikumtuma kwa inu kuti mudziŵe za m'mene tiliri, ndipo kuti adzakulimbitseni mtima. Ndikumtuma pamodzi ndi Onesimo, mbale wathu wokhulupirika ndi wokondedwa, amene ali mmodzi mwa inu. Iwo adzakudziŵitsani zonse zakuno. Aristariko, mkaidi mnzanga, akukupatsani moni. Akuteronso Marko, msuweni wa Barnabasi. Za Markoyo mudalandira kale mau akuti akafika kwanuko, mumlandire bwino. Akutinso moni Yesu, wotchedwa Yusto. Mwa ochokera ku Chiyuda ndi atatu okhaŵa amene akundithandiza pa ntchito ya Ufumu wa Mulungu, ndipo andilimbikitsa kwambiri. Akukupatsani moni Epafra, amene ali mmodzi mwa inu, ndiponso mtumiki wa Khristu Yesu. Nthaŵi zonse iyeyo amalimbikira kukukumbukirani m'mapemphero ake. Amatero pofuna kuti inuyo mukhale okhazikika, angwiro, ndipo kuti muzichilimikira kuchita zonse zimene Mulungu afuna. Ndingathe kumchitira umboni kuti amagwira ntchito kwambiri chifukwa cha inu, ndiponso chifukwa cha anthu okhala ku Laodikea ndi ku Hierapoli. Luka, sing'anga wathu wokondedwa, ndiponso Dema, onsewo akuti moni. Mutiperekereko moni kwa abale athu okhala ku Laodikea, ndiponso kwa Nimfa ndi kwa ampingo amene amasonkhana kunyumba kwake. Kalatayi itaŵerengedwa pakati panu, ikaŵerengedwenso mu mpingo wa ku Laodikea. Ndipo inunso muŵerengeko kalata imene a ku Laodikea adzakutumizirani. Uzani Arkipo kuti, “Samala bwino kuti ntchito imene Ambuye adakupatsa uziigwira moikapo mtima.” Ndi dzanja langalanga ndikulemba mau aŵa: “Moni. Ndine Paulo.” Kumbukirani kuti ndili m'maunyolo. Mulungu akukomereni mtima. Ndife, Paulo, Silivano ndi Timoteo. Tikulembera mpingo wa ku Tesalonika, umene uli wake wa Mulungu Atate, ndiponso wa Ambuye Yesu Khristu. Mulungu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere. Timathokoza Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu nonse ndi kumakutchulani m'mapemphero athu. Timakumbukira kosalekeza pamaso pa Mulungu Atate athu za m'mene mumatsimikizira chikhulupiriro chanu mwa ntchito zanu, za m'mene chikondi chanu chimakuthandizirani kugwira ntchito kolimba, ndiponso za m'mene mumachitira khama poyembekeza Ambuye athu Yesu Khristu. Abale athu, inu amene Mulungu amakukondani, tikudziŵa kuti Iye adakusankhani kuti mukhale ake. Paja Uthenga Wabwino umene tidadza nawo kwa inu sunali wapakamwa chabe, koma tinkaulalika ndi mphamvu za Mzimu Woyera ndiponso mosakayika konse. Mukudziŵa m'mene tinkakhalira pakati panu pofuna kuti tikuthandizeni. Inu mwakhala mukutsata chitsanzo chathu ndi cha Ambuye. Ngakhale mudapeza masautso ambiri, mudalandira mau athu mwa chimwemwe chochokera kwa Mzimu Woyera. Motero nanunso mudakhala chitsanzo kwa okhulupirira onse a ku Masedoniya ndi a ku Akaiya. Inde kuchokera kwa inu mau a Ambuye adakafika ku Masedoniya ndi ku Akaiya, ndipo kuwonjezera apo mbiri yakuti mudakhulupirira Mulungu idawanda ponseponse. Motero palibe chifukwa chakuti ife nkunenapo kanthu. Iwo amakamba okha za m'mene mudatilandirira, ndi za m'mene mudasiyira mafano ndi kutembenukira kwa Mulungu weniweni wamoyo, kuti muzimtumikira. Tsopano mukudikira Mwana wake kuti abwerenso kuchokera Kumwamba. Mwana wakeyo ndi Yesu, amene Mulungu adamuukitsa kwa akufa. Iyeyo amatipulumutsa ku mkwiyo umene ulikudza. Abale, inu nomwe mukudziŵa kuti kucheza kuja tidadzacheza kwanuku, kunali kwaphindu. Monga mukudziŵa, paja nthaŵi imene ija nkuti anthu a ku Filipi atatizunza kale ndi kutichita chipongwe. Komabe Mulungu wathu adatilimbitsa mtima mpaka tidakulalikirani ndithu Uthenga wake Wabwino, ngakhale ambiri ankatsutsana nafe. Pakuti zimene timalalika sitizilalika chifukwa chofuna kuphunzitsa zonama, kapena kuganiza zoipa, kapena kufuna kunyenga anthu ai. Koma timalalika chifukwa Mulungu adativomereza natisungiza Uthenga Wabwino kuti tiulalike. Choncho tikamaphunzitsa sitifuna kukondweretsa anthu, koma timafuna kukondweretsa Mulungu, amene amapenyetsetsa mitima yathu. Monga mukudziŵa, sitidabwere kwanuko ndi mau oshashalika kapena ndi mtima womangofuna phindu. Apo Mulungu angathe kutichitira umboni. Sitinkafunanso ulemu wochokera kwa anthu, kapena kwa inu, kapena kwa ena, ngakhale kunali kotheka kukulamulani kuti mutithandize, popeza kuti ndife atumwi a Khristu. Koma tidakhala ofatsa pakati panu ngati mai wosamalira ana ake. Tinkakukondani, ndipo chifukwa cha kukulakalakani kwambiri, tidatsimikiza zogaŵana nanu osati Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso ngakhale moyo wathu womwe. Abale, simukumbukira nanga kuti tinkagwira ntchito kwambiri mpaka kutopa? Monse muja tinkakulalikirani Uthenga Wabwino wa Mulungu, tinkagwira ntchito zamanja usana ndi usiku, kuwopa kuti tingavutitse wina aliyense mwa inu. Inu ndinu mboni, Mulungu yemwe ndi mboninso, kuti mkhalidwe wathu pakati pa inu okhulupirira unali wangwiro, wolungama, ndi wopanda cholakwa. Paja mukudziŵa kuti, tinkasamala aliyense mwa inu monga momwe amachitira bambo ndi ana ake. Tinkakulimbitsani mtima, kukuthuzitsani mtima ndi kukupemphani kuti mayendedwe anu akhale okomera Mulungu, amene amakuitanani kuti mukaloŵe mu Ufumu wake waulemerero. Pa mbali yathu, timathokoza Mulungu kosalekeza. Timatero chifukwa chakuti pamene mudamva mau a Mulungu amene tidakulalikirani, mudaŵalandira osati ngati mau a anthu chabe, koma monga momwe aliri ndithu, mau a Mulungu. Mauwo ndi omwe akugwira ntchito mwa inu okhulupirira. Abale, zimene zidakugwerani inu ndi zomwe zidagweranso mipingo ya Mulungu ya mwa Khristu Yesu imene ili ku Yudeya. Paja inunso anthu akwanu adakuzunzani monga momwe Ayuda adazunzira akhristu a ku Yudeya. Ayudawo ndi amene adapha Ambuye Yesu ndi aneneri akale, ndipo adatizunza ifenso kwambiri. Ameneŵa sakondweretsa Mulungu konse, ndipo amadana ndi anthu onse. Iwowotu amatiletsa kulalika Uthenga Wabwino kwa anthu a mitundu ina woŵathandiza kuti apulumuke. Motero nthaŵi zonse amanka nawonjezerawonjezera machimo ao, mwakuti tsopano mkwiyo wa Mulungu waŵagwera. Abale, pamene tidasiyana nanu ngakhale kanthaŵi pang'ono, tinkalakalaka kwambiri kuwonana nanunso maso ndi maso. Ngakhale tinkachoka, mtima wathu unali nanube. Nchifukwa chake tidaayesetsa kubweranso kwanuko. Ineyo Paulo, ndidaayesa kangapo, koma Satana adaatilepheretsa. Kodi pamaso pa Ambuye athu Yesu, nchiyani chidzakhale chiyembekezo chathu, chimwemwe chathu, ndi mphotho yoti ife tidzanyadire, Iye akadzabweranso? Si ndinu nomwe nanga? Pajatu ulemu wathu ndi chimwemwe chathu ndinu amene. Nchifukwa chake pamene sitidathenso kupirira, tidalolera kutsalira tokha ku Atene. Choncho tidatuma Timoteo, mbale wathu ndi mnzathu wogwira naye ntchito ya Mulungu yolalika Uthenga Wabwino wa Khristu. Tidamtuma kuti adzakulimbitseni mtima ndi kukukhazikitsani m'chikhulupiriro chanu, kuwopa kuti wina aliyense mwa inu angagwedezeke chifukwa cha mazunzoŵa. Mukudziŵa nokha kuti Mulungu ndiye adalola kuti zimenezi zitigwere. Pajatu pamene tinali pamodzi nanu, tidaakuuziranitu kuti tidzayenera kuzunzidwa. Ndipo monga mukudziŵa, zimenezi zidachitikadi. Nchifukwa chake, pamene sindidathenso kupirira, ndidatuma Timoteo kuti adzaone m'mene chiliri chikhulupiriro chanu. Pakuti ndinkaopa kuti kapena Satana, Wonyenga uja, adakunyengani, ndipo kuti ntchito zathu zonse pakati panupo zidangopita pachabe. Koma tsopano Timoteo wabwerako kuchokera kwanuko, ndipo watisimbira mbiri yokoma ya chikhulupiriro chanu ndi chikondi chanu. Watiwuzanso kuti masiku onse mumatikumbukira mokondwa, ndipo kuti mumalakalaka kutiwona ife, monga momwe ifeyo timafunitsitsira kukuwonaninso inuyo. Motero abale, pakati pa masautso ndi mazunzo athu onse, chikhulupiriro chanu chatithuzitsa mtima. Takhalanso ndi moyo tsopano pakuti mukulimbika pa chikhristu chanu. Nanga tingathe bwanji kuyamika Mulungu mokwanira chifukwa cha inu, poona chimwemwe chonse chimene tili nacho pamaso pa Mulungu wathu? Ndi mtima wonse timapemphera usana ndi usiku kuti tiwonane nanunso maso ndi maso, kuti tikakwaniritse zimene zikusoŵa pakuwonetsa chikhulupiriro chanu. Tikupempha kuti Mulungu Atate athu mwini, ndi Ambuye athu Yesu atikonzere njira yabwino kuti tidzafike kwanuko. Ambuye akulitsirekulitsire kukondana kwanu, ndiponso chikondi chanu cha pa anthu onse, monga momwe chikondi chathu cha pa inu chikukulirakulira. Motero Iye adzalimbitsa mitima yanu kuti idzakhale yangwiro ndi yoyera pamaso pa Mulungu Atate athu, pamene Ambuye Yesu adzabwerenso pamodzi ndi oyera ake onse. Potsiriza tsono, abale, tifuna tikupempheni kanthu. Mudalandira kwa ife mau onena za m'mene muziyendera kuti mukondweretse Mulungu. Mukutsata mayendedwe otere kumene, koma tikukupemphani kolimba m'dzina la Ambuye Yesu kuti muchite zimenezi koposa kale. Pakuti mukudziŵa malangizo amene tidakupatsani ochokera kwa Ambuye Yesu. Chimene Mulungu akufuna ndi ichi: mukhale oyera mtima, ndiye kuti muzipewa dama. Aliyense mwa inu adziŵe kulamula thupi lake, pakulilemekeza ndi kulisunga bwino, osalidetsa. Musamangotsata zilakolako zonyansa, monga amachitira akunja, amene sadziŵa Mulungu. Pa zimenezi munthu asachimwire mbale wake kapena kumpezera. Monga tidakuuzani kale monenetsa, Ambuye adzalanga anthu onse ochita zotere. Paja Mulungu sadatiitane kuti tizichita zonyansa, koma kuti tikhale oyera mtima. Motero munthu wokana mau ameneŵa, sakukana munthu chabe ai, koma akukana Mulungu amene amakupatsani Mzimu wake Woyera. Kunena za kukondana pakati pa akhristu, nkosafunikira kuti ndichite kukulemberani, popeza kuti ndi Mulungu mwini amene adakuphunzitsani za m'mene muyenera kukonderana. Ndipo mumakondana nawodi abale onse a m'dziko lonse la Masedoniya. Koma tikukupemphani abale, kuti muchite zimenezi koposa kale. Yesetsani kukhala ndi moyo wabata. Aliyense asamale ntchito yakeyake ndi kumagwira ntchito ndi manja ake. Chitani zimenezi, monga tidakulangizirani muja, kuti akunja azikulemekezani, ndi kuti inuyo mukhale osadalira wina aliyense. Abale, tifuna kuti mudziŵeko za anthu amene adamwalira, kuti chisoni chanu chisakhale ngati cha anthu ena amene alibe chiyembekezo. Paja ife timakhulupirira kuti Yesu adaamwalira naukanso. Motero timakhulupiriranso kuti anthu amene adamwalira akukhulupirira Yesu, iwonso Mulungu adzaŵaukitsa nkubwera nawo pamodzi ndi Yesuyo. Tsopano tikuuzeni mau a Ambuye mwini. Ife amoyofe, otsala mpaka kubwera kwa Ambuye, sikuti tidzaŵasiya kumbuyo amene adamwalira aja ai. Padzakhala mfuu wa mau a mngelo wamkulu ndi wa lipenga la Mulungu. Ndipo pamenepo Ambuye mwini adzatsika kuchokera Kumwamba. Anthu amene adafa akukhulupirira Khristu, adzayamba ndiwo kuuka. Pambuyo pake ife amoyofe, otsalafe, tidzatengedwa pamodzi nawo m'mitambo kuti tikakumane ndi Ambuye mu mlengalenga. Motero tidzakhala ndi Ambuye nthaŵi zonse. Nchifukwa chake tsono muzithuzitsana mtima pokambirana zimenezi. Komatu abale, za nthaŵi ndi nyengo yake yodzachitika zimenezi, nkosafunikira kuti ndichite kukulemberani. Inu nomwe mukudziŵa bwino kuti tsiku la Ambuye likadzafika ngati mbala yausiku. Pamene anthu azikati, “Pali mtendere, tili pabwino”, pamenepo chiwonongeko chidzaŵagwera modzidzimutsa. Chidzaŵadzidzimutsa monga momwe zoŵaŵa zimamchitira mkazi pa nthaŵi yoti achire; ndipo sadzatha konse kuchizemba. Koma inu abale, simuli m'chimbulimbuli kuti tsikulo nkukudzidzimutsani ngati mbala. Paja nonsenu zanu zonse ndi zam'kuŵala, ndiye kuti zausana. Ife zathu si zausiku kapena zamumdima ai. Nchifukwa chake tsono tisagone tulo monga momwe amachitira anthu ena, ife tikhale maso, tikhale osaledzera. Anthu ogona tulo, amagona usiku, anthu oledzera amaledzera usiku. Koma ife, popeza kuti zathu nzausana, tisamaledzera. Tikhale titavala chikhulupiriro ndi chikondi ngati chovala chachitsulo chapachifuwa. Ndipo ngati chisoti choteteza kumutu tivale chiyembekezo chakuti tidzapulumuka. Paja Mulungu sadatisankhe kuti tidzaone mkwiyo wake, koma kuti tidzalandire chipulumutso kwa Ambuye athu Yesu Khristu. Iwo adatifera kuti tikakhale ndi moyo pamodzi naye, ngakhale pamene tili amoyo kapena titafa kale. Nchifukwa chake muzilimbitsana mtima ndi kumathandizana, monga momwe mukuchitiramu. Abale, tikukupemphani kuti muziŵalemekeza amene akugwira ntchito pakati panu, amene Ambuye adaŵaika kuti azikutsogolerani ndi kumakulangizani. Mwa chikondi muziŵachitira ulemu kwambiri chifukwa cha ntchito yao. Muzikhalitsana ndi mtendere pakati panu. Abale, tikukupemphani kuti anthu amene amangokhala osafuna kugwira ntchito muziŵadzudzula, anthu otaya mtima muziŵalimbikitsa. Anthu ofooka muziŵathandiza, anthu onsewo muziŵalezera mtima. Onetsetsani kuti wina aliyense mnzake akamchita choipa, asabwezere choipacho. Koma nthaŵi zonse muziyesetsa kuchitira zabwino anzanu ndi anthu ena onse. Khalani okondwa nthaŵi zonse. Muzipemphera kosalekeza. Muzithokoza Mulungu pa zonse. Paja zimene Mulungu amafuna kuti muzichita mwa Khristu Yesu nzimenezi. Musayese kuletsa ntchito ya Mzimu Woyera. Musanyoze mau olalikidwa m'dzina la Mulungu, koma zonse muziziyesa bwino, kuti muwonetsetse ngati nzoona. Musunge zimene zili zabwino, ndipo mupewe choipa cha mtundu uliwonse. Mulungu mwini, amene amatipatsa mtendere, akusandutseni angwiro pa zonse. Akusungeni athunthu m'nzeru, mumtima ndi m'thupi, kuti mudzakhale opanda chilema pobwera Ambuye athu Yesu Khristu. Iye amene akukuitanani ngwokhulupirika, ndipo adzakuchitirani zimenezi. Abale, muzitipempherera. Abale onse muŵapatseko moni mwachikondi. M'dzina la Ambuye ndikukulamulani kuti kalatayi muŵaŵerengere abale onse. Ambuye athu Yesu Khristu akukomereni mtima. Ndife, Paulo, Silivano ndi Timoteo. Tikulembera mpingo wa ku Tesalonika, umene uli wake wa Mulungu Atate, ndiponso wa Ambuye Yesu Khristu. Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere. Tiyenera kuthokoza Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu, abale. Nkoyeneradi kutero, chifukwa chikhulupiriro chanu chikunka chikukulirakulira kwambiri pamodzi ndi kukondana kwanu pakati pa inu nonse. Nchifukwa chake ife timakunyadirani, m'mipingo yonse ya Mulungu, chifukwa cha kulimbika kwanu ndi chikhulupiriro chanu pakati pa masautso ndi mazunzo onse amene adakugwerani. Zonsezi zikutsimikiza kuti Mulungu amaweruza molungama. Cholinga chake nchakuti inu mupezeke oyenera kuloŵa mu Ufumu wa Mulungu umene mukuusaukira tsopano. Paja Mulungu mwa chilungamo chake, adzaŵalanga ndi masautso anthu amene amakusautsani inu. Koma inu amene mukusauka tsopano, adzakupatsani mpumulo pamodzi ndi ife tomwe. Adzachita zimenezi, Ambuye Yesu akadzabwera kuchokera Kumwamba pamodzi ndi angelo ake amphamvu. Adzabwera ndi moto woyaka, nadzalanga anthu amene sadziŵa Mulungu, ndi amene sadamvere Uthenga Wabwino wa Ambuye athu Yesu. Chilango chao nchakuti adzaonongedwa kwamuyaya, sadzaona konse nkhope ya Ambuye kapena ulemerero wa mphamvu zake, pa tsiku limene Iye adzabwera kuti alemekezedwe mwa oyera, ndipo alandire ulemu mwa onse omkhulupirira. Ndipotu inunso mudzakhala nawo, chifukwa mudakhulupirira umboni wathu. Nchifukwa chake timakupemphererani nthaŵi zonse, kuti Mulungu wathu akusandutseni oyenera moyo umene Iye adakuitanirani. Timapemphanso kuti ndi mphamvu zake akulimbikitseni kuchita zabwino zonse zimene mumalakalaka kuzichita, ndiponso ntchito zotsimikizira chikhulupiriro chanu. Motero dzina la Ambuye athu Yesu lidzalemekezedwa mwa inu, ndipo inu mudzalemekezedwa mwa Iye. Zonsezi zidzachitika chifukwa cha kukoma mtima kwa Mulungu wathu ndi kwa Ambuye Yesu Khristu. Pa za kubweranso kwa Ambuye athu Yesu Khristu, ndiponso za kusonkhana kwathu kuti tikakumane naye, tifuna kukupemphani kanthu, abale. Maganizo anu asasokonezeke msanga, ndipo musaopsedwe ndi mau akuti, “Tsiku la Ambuye lafika,” ngakhale anene kuti mauwo ngochokera kwa Mzimu Woyera, kapena kuti taŵanena ndife, kapena tachita kuŵalemba m'kalata. Musalole kuti wina akupusitseni mwa njira iliyonse. Pajatu lisanafike tsikulo, kudzayamba kwachitika zoti anthu ochuluka akupandukira Mulungu, ndipo kudzaoneka Munthu Woipitsitsa uja, woyenera kutayikayu. Ameneyu ndi mdani, ndipo adzadziika pamwamba pa chilichonse chimene anthu amachitcha mulungu kapena amachipembedza, kotero kuti mwiniwakeyo adzadzikhazika m'Nyumba ya Mulungu ndi kudzitcha Mulungu. Kodi simukukumbukira kuti ndinkakuuzani zimenezi muja ndinali kwanuko? Mukudziŵanso chimene chikumletsa kuwoneka tsopano, koma adzaululuka ndithu pa nthaŵi yake. Ngakhale tsopano lomwe lino uchimo wayamba kugwira ntchito mobisika. Koma zoyenera kuchitikazo sizidzachitika mpaka amene akuletsa uchimowo tsopano atayamba wachotsedwa. Tsono pamenepo Munthu Woipitsitsa uja adzaululuka. Ndipo Ambuye Yesu adzamthetsa ndi mpweya wa m'kamwa mwake, nkumuwonongeratu ndi maonekedwe ake aulemerero a kubwera kwake. Munthu Woipitsitsa uja adzabwera ndi mphamvu za Satana. Adzachita zamphamvu zosiyanasiyana, ndiponso zizindikiro ndi zozizwitsa zonyenga. Mwa njira iliyonse adzanyenga anthu amene adzaonongedwa chifukwa chokana kukonda choona chimene chikadaŵapulumutsa. Nchifukwa chake Mulungu adzatumiza mphamvu zoŵasokoneza, kuti akhulupirire zonama. Motero adzalangidwa onse amene sadakhulupirire choona, koma adakondwerera kusalungama. Koma ife tikuyenera kumathokoza Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu, abale, amene Ambuye amakukondani. Paja Mulungu adakusankhani pachiyambi pomwe kuti mupulumuke. Mudapulumuka chifukwa Mzimu Woyera adakusandutsani anthu akeake a Mulungu, ndipo mudakhulupirira choona. Mulungu adakuitanirani zimenezi kudzera mwa Uthenga Wabwino umene tidakulalikirani. Adakuitanani kuti mulandire nao ulemerero wa Ambuye athu Yesu Khristu. Tsono abale, khalani olimbika, ndipo mugwiritse miyambo imene tidakuphunzitsani ndi mau apakamwa kapena am'makalata. Mulungu Atate athu adatikonda, ndipo mwa kukoma mtima kwake adatipatsa kulimba mtima kosatha ndi chiyembekezo chokoma. Iye pamodzi ndi Yesu Khristu Ambuye athu athuzitse mitima yanu ndi kukupatsani mphamvu za kuchita ndi kulankhula zabwino zilizonse. Potsiriza, abale, mutipempherere kuti mau a Ambuye afalikire msanga, ndipo anthu aŵalandire mauwo mwaulemu, monga momwe mudachitira inu. Mupempherenso kuti Mulungu atipulumutse kwa anthu ovuta ndi oipa, pakuti si onse ali ndi chikhulupiriro. Koma Ambuye ngokhulupirika, ndipo adzakulimbitsani mtima ndi kukutchinjirizani kwa Woipa uja. Ambuye amatipatsa chikhulupiriro chakuti mukuchita zonse zimene timakuuzani, ndipo kuti mudzazichitabe. Ambuye aongolere maganizo anu kuti muziyenda m'chikondi cha Mulungu, ndikutsata khama la Khristu. Abale, tsopano tikukulamulani m'dzina la Ambuye Yesu Khristu kuti muziŵapewa abale onse a makhalidwe aulesi, osafuna kutsata mwambo umene tidaŵapatsa. Paja inu nomwe mukudziŵa zimene muyenera kuchita pofuna kutitsanzira. Ife sitinali aulesi pamene tinali pakati panu. Sitidalandire chakudya kwa munthu aliyense osalipira, koma tidagwira ntchito kwambiri usana ndi usiku mpaka kutopa, kuwopa kuti tingalemetse wina aliyense mwa inu. Sitidachitetu zimenezi chifukwa choti tilibe mphamvu zopemphera chithandizo kwa inu, koma tinkafuna kukhala chitsanzo choti muzichitsanzira. Paja nthaŵi imene tinali nanu pamodzi, tidaakulamulani kuti munthu wosafuna kugwira ntchito, kudyanso asadye. Tikunena zimenezi popeza kuti tikumva kuti pali ena pakati panu amene ali ndi khalidwe laulesi. Anthu ameneŵa sagwira ntchito konse, koma amangoloŵera pa za anzao. M'dzina la Ambuye Yesu Khristu tikuŵalamula ndi kuŵachenjeza anthu otere kuti azigwira ntchito mwabata, ndi kumadya chakudya chodzigwirira ntchito. Koma inu abale, musatope nkuchita zabwino. Ngati wina aliyense akana kumvera mau amene talemba m'kalatayi, mumuwonetsetse ameneyo, ndipo musayanjane naye, kuti choncho achite manyazi. Koma musamuwone ngati mdani. Makamaka mumchenjeze ngati mbale. Ambuye, eniake mtendere amene, akupatseni mtenderewo nthaŵi zonse mwa njira iliyonse. Ambuye akhale ndi inu nonse. Ndi dzanja langa ndikulemba mau aŵa: “Moni. Ndine, Paulo.” Mauŵa ndi chizindikiro changa m'kalata iliyonse. Ndimalemba motero. Ambuye athu Yesu Khristu akukomereni mtima nonse. Ndine, Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu, monga adalamulira Mulungu, Mpulumutsi wathu, ndiponso Khristu Yesu, chiyembekezo chathu. Ndikulembera iwe Timoteo, mwana wanga weniweni m'chikhulupiriro. Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Ambuye athu akukomere mtima, akuchitire chifundo ndi kukupatsa mtendere. Pamene ndinkanyamuka kupita ku Masedoniya, paja ndidaakupempha kuti ukhalire ku Efeso. Kuli anthu ena kumeneko amene akuphunzitsa zina zachilendo, ndiye ndikufuna kuti iweyo uŵaletse. Uŵauze kuti aleke kumangoika mtima pa nthano zopeka, ndi pa kufufuza kosalekeza dongosolo la maina a makolo. Zimenezi zimangoutsa mikangano chabe, siziphunzitsa konse zimene Mulungu adakonzeratu, zomwe zimadziŵika pakukhulupirira. Cholinga changa pokupatsa malangizo ameneŵa, nchakuti pakhale chikondi chochokera mu mtima woyera, mu mtima wopanda kanthu koutsutsa, ndiponso m'chikhulupiriro chopanda chiphamaso. Anthu ena adapatuka pa zimenezi, ndipo adasokera nkumatsata nkhani zopanda pake. Iwo amafuna kukhala aphunzitsi a Malamulo a Mulungu, chonsecho samvetsa zimene iwo omwe akunena kapena zimene akufuna kutsimikiza. Tikudziŵa kuti Malamulo ngabwino, malinga nkuŵagwiritsa ntchito moyenera. Koma mumvetsetse kuti saika malamulo chifukwa cha anthu olungama, koma chifukwa cha anthu osamvera, ndi osaweruzika, anthu ochimwa ndi osapembedza, monga anthu opha atate ao, amai ao, kapena anthu ena. Malamulo amaŵaika chifukwa cha anthu adama, ochimwa ndi amuna anzao, oba anthu, amabodza, olumbira monama, ndi ochita chilichonse chotsutsana ndi chiphunzitso choona. Chiphunzitso choonacho chimapezeka mu Uthenga Wabwino wonena za ulemerero wa Mulungu wolemekezeka, umene Iye mwini adandisungiza. Ndikuthokoza Khristu Yesu Ambuye athu, amene adandipatsa mphamvu pa ntchitoyi. Ndikumthokoza pondiwona wokhulupirika nandipatsa ntchito yomtumikira, ngakhale kuti kale ndinkamuchita chipongwe, kumzunza ndi kumnyoza. Koma Mulungu adandichitira chifundo chifukwa ndinkazichita mosadziŵa, poti ndinali wopanda chikhulupiriro. Ambuye athu adandikomera mtima koposa, nkundipatsa chikhulupiriro ndi chikondi zimene tili nazo chifukwa chogwirizana ndi Khristu Yesu. Aŵa ndi mau otsimikizika, oyenera kuŵavomereza ndi mtima wonse, akuti Khristu Yesu adabwera pansi pano kuti adzapulumutse anthu ochimwa. Ndipo mwa iwowo ine ndiye wochimwa koposa. Koma Mulungu adandichitira chifundo, kuti mwa ine, wochimwa koposane, Khristu Yesu aonetse kuleza mtima kwake konse. Adafuna kuti ndikhale chitsanzo cha kuŵalezera mtima onse amene adzamkhulupirire kuti alandire moyo wosatha. Kwa Mfumu yamuyaya, yosafa, yosaoneka, amene Iye yekha ndiye Mulungu, kukhale ulemu ndi ulemerero mpaka muyaya. Amen. Iwe Timoteo, mwana wanga, ndikukupatsa malangizo ameneŵa molingana ndi zimene aneneri adaanenapo kale za iwe. Mau amenewo akuthandize kumenya nkhondo yabwino, uli ndi chikhulupiriro ndiponso ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa. Ena sadamvere pamene mtima wao unkaŵatsutsa, motero chikhulupiriro chao chidaonongeka. Mwa iwowo wina ndi Himeneo, wina Aleksandro, anthu amene ndaŵapereka kwa Satana kuti aphunzire kusanyoza Mulungu mwachipongwe. Tsono choyamba ndikukupemphani kuti pakhale mapemphero opempherera anthu onse. Mapemphero ake akhale opemba, opempha ndi othokoza Mulungu. Muziŵapempherera mafumu ndi onse amene ali ndi ulamuliro, kuti tikhale ndi moyo wabata ndi wamtendere, tizitamanda Mulungu pa zonse ndi kumadzilemekeza. Zimenezi nzabwino ndi zokondweretsa pamaso pa Mulungu, Mpulumutsi wathu. Iye amafuna kuti anthu onse apulumuke ndipo kuti adziŵe choona. Pajatu Mulungu ndi mmodzi yekha, Mkhalapakati mmodzi yekhanso pakati pa Mulungu ndi anthu, munthu uja timati Khristu Yesu. Iyeyo adadzipereka kuti akhale momboli wa anthu onse. Umenewu unali umboni umene udaperekedwa pa nthaŵi yake. Nchifukwa chake ine adandiika kuti ndikhale mlaliki wake ndiponso mtumwi, wophunzitsa anthu a mitundu ina mau a chikhulupiriro choona. Sindikunamatu ai, ndikunena zoona. Ndikufuna kuti paliponse amuna popemphera azikweza manja ao kwa Mulungu momchitira ulemu, mopanda mkwiyo kapena kukangana. Ndikufunanso kuti akazi azivala mwaulemu, mwanzeru ndi moyenera. Inde adzikongoletse, komatu osati ndi tsitsi lochita kukonza monyanyira, kapena ndi zokongoletsa zagolide, kapena mikanda yamtengowapatali, kapena zovala zamtengowapatali. Kwenikweni adzikongoletse ndi ntchito zabwino, monga ayenera kuchitira akazi amene amati ndi opembedza Mulungu. Akazi pophunzitsidwa, azikhala chete ndi a mtima wodzichepetsa. Sindilola kuti mkazi aziphunzitsa kapena kukhala ndi ulamuliro pa amuna. Mkazi kwake nkukhala chete. Paja Adamu ndiye adaayambira kulengedwa, pambuyo pake Heva. Ndiponso si Adamu amene adaanyengedwa, koma mkaziyo ndiye adaanyengedwa, naphwanya lamulo la Mulungu. Koma mkazi adzapulumukabe kudzera m'kubala ana, malinga akalimbikira modzichepetsa m'chikhulupiriro, m'chikondi ndi m'kuyera mtima. Aŵa ndi mau otsimikizika ndithu akuti, “Ngati munthu afuna ntchito ya kuyang'anira Mpingo, akukhumba ntchito yaulemu.” Woyang'anira Mpingo azikhala munthu wopanda chokayikitsa, akhale wa mkazi mmodzi yekha, akhale wodzigwira, wa maganizo anzeru, waulemu, wosamala bwino alendo, ndi wotha kuphunzitsa. Asakhale chidakwa, asakhale wandeu, koma wofatsa, wosakangana ndi anthu, ndi wosakonda ndalama. Akhale wodziŵa kuyendetsa bwino banja lake, ndi kulera bwino ana ake, kuti akhale omvera ndi aulemu kwenikweni. Ngati munthu sadziŵa kuyendetsa bwino banja lake, nanga angasunge bwanji Mpingo wa Mulungu? Asakhale munthu wolandiridwa mu mpingo chatsopano, kuwopa kuti angadzitukumule nkulangidwa monga momwe Satana adalangidwira. Kuwonjezera pamenepo, akhale munthu woti ndi akunja omwe amamlemekeza, mwinamwina nkudzayamba kunyozedwa nagwa mu msampha wa Satana. Chimodzimodzinso ndi atumiki a mpingo: akhale ochita zachiukulu, osanena paŵiripaŵiri, osakhala ozoloŵera zoledzeretsa, osakonda udyo phindu la ndalama. Akhale anthu a mtima wopanda kanthu koutsutsa posunga zoona za chikhulupiriro zimene Mulungu adaulula. Iwonso ayambe ayesedwa, ndipo pambuyo pake, ngati alibe chokayikitsa, ndiye asenze udindo wa atumiki. Momwemonso akazi akhale ochita zachiukulu, osasinjirira, odzigwira, ndi okhulupirika pa zonse. Atumiki a mpingo akhale a mkazi mmodzi yekha. Akhale olera ana ao bwino, oyendetsanso bwino mabanja ao. Paja anthu ogwira bwino ntchito ya utumiki, amadzitengera mbiri yabwino, ndipo amalimba mtima kwenikweni pakuika chikhulupiriro chao mwa Khristu Yesu. Pamene ndikukulembera zimenezi, ndikuyembekeza kudzafika kwanuko posachedwa. Koma zina zikandichedwetsa, zimene ndanenazi zidzakudziŵitsa za m'mene anthu ayenera kukhalira m'banja la Mulungu, limene lili Mpingo wa Mulungu wamoyo, ndi mzati wochirikiza choona. Ndithudi, chinsinsi cha chipembedzo chathu nchachikulu: “Iye uja adaonekera ali ndi thupi la munthu, Mzimu Woyera adamchitira umboni kuti ndi wolungama, angelo adamuwona, adalalikidwa pakati pa anthu a mitundu yonse, anthu a pa dziko lonse lapansi adamkhulupirira, Iyeyo adatengedwa kunka kumwamba mu ulemerero.” Mzimu Woyera akunena momveka kuti pa masiku otsiriza anthu ena adzataya chikhulupiriro chao. Adzamvera mizimu yonyenga ndi zophunzitsa zochokera kwa mizimu yoipa. Zophunzitsa zimenezi nzochokera ku chinyengo cha anthu onama, amene mumtima mwao adalembedwa chizindikiro ndi chitsulo chamoto. Iwo amaletsa anthu ukwati, nkumaŵalamula kusala zakudya zina. Koma tsono zakudyazo Mulungu adazilenga kuti amene ali okhulupirira ndi odziŵa choona, azidye moyamika Mulungu. Pajatu chilichonse chimene Mulungu adalenga nchabwino, palibe chilichonse choti munthu asale, akamachilandira moyamika Mulungu, pakuti chimayeretsedwa ndi mau a Mulungu ndi mapemphero aja. Ngati abale uŵalangiza zimenezi, udzakhala mtumiki wabwino wa Khristu Yesu, woleredwa ndi mau a chikhulupiriro ndi a chiphunzitso choona chimene wakhala ukutsata. Koma upewe nthano zachabe, monga zimene akazi okalamba amakonda kukamba. Udzizoloŵeze kukhala ndi moyo wolemekeza Mulungu. Kuzoloŵeza thupi kumapindulitsapo pang'ono, koma moyo wolemekeza Mulungu umapindulitsa pa zonse. Umatilonjeza moyo pa moyo uno ndiponso pa moyo wakutsogolo. Ameneŵa ndi mau otsimikizika oyenera kuŵavomereza ndi mtima wonse. Nchifukwa chake timagwira ntchito kolimba, ndipo timayesetsa kupambana, pakuti chiyembekezo chathu chili pa Mulungu wamoyo, amene ali Mpulumutsi wa anthu onse, makamaka okhulupirira Khristu. Uzilamula ndi kuphunzitsa zimenezi. Munthu asakupeputse poona kuti ndiwe wachinyamata, koma ukhale chitsanzo kwa akhristu onse pa mau, pa mayendedwe, pa chikondi, pa chikhulupiriro ndi pa kuyera mtima. Mpaka pamene ndidzabwere, uchite khama kuŵerengera anthu mau a Mulungu, kuŵalalikira ndi kuŵaphunzitsa. Usanyozere mphatso yaulere ija ili mwa iweyi, imene udailandira kudzera m'mau otchulidwa m'dzina la Mulungu, pamene gulu la akulu a Mpingo lidaakusanjika manja. Ntchito zimenezi uzizichita mosamala ndi modzipereka, kuti anthu onse aone kuti moyo wako wautumiki ukukulirakulira. Udziyang'anire bwino wekha, ndi kusamala zimene umaphunzitsa. Ulimbikire kutero, chifukwa pakuchita zimenezi udzadzipulumutsa iwe wemwe, ndiponso anthu amene amamva mau ako. Munthu wachikulire usamdzudzule mokalipa, koma umchenjeze monga ngati bambo wako. Amuna achinyamata uzikhalitsana nawo ngati abale ako. Azimai achikulire uzikhalitsana nawo ngati amai ako, ndipo azimai a zaka zochepa uzikhalitsana nawo ngati alongo ako, m'kuyera mtima kwenikweni. Uziŵachitira ulemu azimai amasiye, amenetu ali amasiye enieni. Koma ngati mai wamasiye ali ndi ana kapena adzukulu, anawo ayambe aphunzira kukwaniritsa udindo wao pa banja lao moopa Mulungu, kuti pakutero abwezere makolo ao zimene adalandira kwa iwo. Pakuti zimenezi Mulungu amakondwera nazo akamaziwona. Mai amene ali wamasiye kwenikweni, wopanda wina aliyense womsamala, ameneyo waika chiyembekezo chake pa Mulungu, ndipo amapemphera kosalekeza usana ndi usiku kuti Mulungu azimthandiza. Koma mai wamasiye amene amangodzisangalatsa ndi zapansipano, ameneyo wafa kale ngakhale akali moyo. Uziŵalamula zimenezi, kuti akhale opanda mlandu. Ngati wina aliyense saŵapatsa zofunika achibale ake, makamaka a m'banja mwake momwe, ameneyo wataya chikhulupiriro chake, ndipo kuipa kwake nkoposa kwa munthu wosakhulupirira. Wina aliyense asaloledwe kuloŵa m'gulu la azimai amasiye, asanakwanitse zaka 60. Akhale woti adakwatiwapo ndi mwamuna mmodzi yekha. Akhale mai woti anthu amamchitira umboni wakuti amachitadi ntchito zabwino. Akhale woti ankalera ana ake bwino, ankalandira bwino alendo, ankasambitsa mapazi a anthu a Mulungu, ndipo ankathandiza anthu amene anali m'mavuto. Akhalenso mai woti ankadzipereka pa ntchito zonse zabwino. Koma azimai amasiye a zaka zochepera uzikana kuŵalemba m'gulu limeneli. Pajatu zilakolako zao zikayamba kuŵavutitsa nkuŵalekanitsa ndi Khristu, amangofuna kukwatiwanso. Pamenepo amapezeka olakwa, chifukwa chosasunga lonjezo lao loyamba. Kuwonjezera pamenepo, amagwa m'chizoloŵezi cha kungokhala khale, motero amangoyendayenda ku nyumba za anthu. Tsonotu samangokhala khale chabe ai, amachitanso miseche nkumaloŵera za eni, ndi kukhala omalankhula zimene samayenera kulankhula. Nchifukwa chake nkadakonda kuti azimai amasiye a zaka zochepera azikwatiwanso, abale ana, ndipo azisamala bwino panyumba pao, kuti adani athu asapeze mpata wotisinjirira. Paja alipo kale azimai amasiye ena amene adapatukapo nkumatsata Satana. Koma ngati mai wina aliyense wachikhristu ali ndi achibale amene ali azimai amasiye, aziŵasamala iyeyo, osasenzetsa mpingo katundu wakeyo. Motero mpingo udzatha kusamala azimai amasiye opanda oŵathandiza. Akulu a mpingo otsogolera mpingo bwino, akhale oyenera kuŵalemekeza moŵirikiza, makamaka amene amagwira ntchito yolalika mau a Mulungu ndiponso yophunzitsa. Paja Malembo akuti, “Usaimange pakamwa ng'ombe imene ikupuntha tirigu.” Penanso akuti, “Wantchito ngwoyenera kulandira malipiro ake.” Usamamvere mau oneneza mkulu wa mpingo, pokhapokha ngati pali mboni ziŵiri kapena zitatu. Opitirirabe kuchimwa uziŵadzudzula pamaso pa onse, kuti ena onsewo achite mantha. Pamaso pa Mulungu, pamaso pa Khristu Yesu, ndi pamaso pa angelo onse osankhidwa, ndikukulamula ndithu kuti uzitsata malamulo ameneŵa mopanda tsankho, ndipo kuti usachite chilichonse mokondera. Usafulumire kumsanjika manja munthu, ndipo usavomerezane ndi anthu ena pa uchimo wao. Iwe usunge bwino kuyera mtima kwako. Uleke kumangomwa madzi okha. Koma uzimwako vinyo pang'ono, paja umavutika ndi m'mimba, ndiponso chifukwa cha kudwaladwala kwako kuja. Pali anthu ena amene machimo ao amaonekeratu poyera asanakambe nkomwe mlandu wao, m'menemo ena machimo ao amayamba kudziŵika pokamba mlandu. Momwemonso ntchito zokoma zimaonekera poyera, ndipo ngakhale zipande kutero, sizingathe kubisika nthaŵi zonse. Onse amene ali mu ukapolo aziwona ambuye ao ngati oyenera kuŵachitira ulemu ndithu, kuti anthu anganyoze dzina la Mulungu ndiponso zimene timaphunzitsa. Amene ambuye ao ndi akhristu, asaŵapeputse poona kuti ndi abale. Kwenikweni aziŵatumikira koposa, popeza kuti amene amapindula ndi ntchito yao, nawonso ndi akhristu, ndiponso okondedwa. Uziŵaphunzitsa anthu ndi kuŵalamula ntchito zimenezi. Angathe kupezeka munthu wophunzitsa zosiyana ndi zimenezi, wosavomereza mau oona a Ambuye athu Yesu Khristu ndi chiphunzitso chogwirizana ndi moyo wolemekeza Mulungu. Munthu wotere ndi wodzitukumula ndi kunyada, sadziŵa kanthu. Mtima wake ngwodwala, wongofuna zotsutsanatsutsana ndi kukangana pa mau chabe. Zimenezi zimabweretsa kaduka, kusamvana, kusinjirirana, kuganizirana zoipa, kupsetsana mtima kosalekeza pakati pa anthu amene nzeru zao zidaonongekeratu ndipo sazindikiranso choona. Iwo amayesa kuti kupembedza Mulungu ndi njira yopatira chuma. Nzoonadi, kupembedza Mulungu kumapindulitsa kwambiri, malinga munthu akakhutira ndi zimene ali nazo. Sitidatenge kanthu poloŵa m'dziko lino lapansi, ndipo sitingathenso kutenga kanthu potulukamo. Tsono ngati tili ndi chakudya ndi zovala, zimenezi zitikwanire. Koma anthu ofuna kulemera, amagwa m'mayeso, amagwidwa mu msampha wa zilakolako zambiri zopusa ndi zoononga. Zilakolakozo zimamiza anthu m'chitayiko choopsa. Pajatu kukonda ndalama ndi gwero la zoipa zonse. Chifukwa cha kuika mtima pa ndalama anthu ena adasokera, adasiya njira ya chikhulupiriro, ndipo adadzitengera zoŵaŵitsa mitima. Koma iwe, munthu wa Mulungu, uzipewe zonsezi. Uzikhala ndi mtima wofunafuna chilungamo, wolemekeza Mulungu, wokhulupirika, wachikondi, wolimbika ndi wofatsa. Uzimenya nkhondo yabwino ya kusunga chikhulupiriro, mpaka ukalandire moyo wosatha. Paja Mulungu adakuitanira zimenezi, ndipo udavomera bwino chikhulupiriro chako pamaso pa mboni zambiri. Ndikukulamula pamaso pa Mulungu amene amapatsa moyo zinthu zonse, ndiponso pamaso pa Khristu Yesu amene popereka umboni pamaso pa Ponsio Pilato, adaanena zoona zenizeni. Ndikukulamula kuti, mopanda cholakwa kapena chokayikitsa, utsate bwino zonse zimene udalamulidwa, mpaka Ambuye athu Yesu Khristu adzabwerenso. Pa nthaŵi yake Mulungu adzamuwonetsa kwa ife. Mulunguyo ngwodala ndipo Iye yekha ndiye Wolamula, ndiye Mfumu ya mafumu onse, ndiponso Mbuye wa ambuye onse. Ndiye yekha wosafa, ndipo amakhala m'kuŵala kosayandikizika. Chikhalire palibe munthu amene adamuwona, palibenso amene angathe kumuwona. Kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu mpaka muyaya. Amen. Anthu amene ali olemera pa zinthu zapansipano, uŵalamule kuti asanyade kapena kudalira chuma chimene sichidziŵika ngati chidzakhalitsa. Koma azidalira Mulungu amene amatipatsa zonse moolowa manja kuti tisangalale nazo. Uŵalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pa ntchito zabwino, oolowa manja, ndi okonda kugaŵana zinthu zao ndi anzao. Pakutero adzadziwunjikira chuma chokoma ndi chokhalitsa chimene chidzaŵathandize kutsogoloko, kuti akalandire moyo umene uli moyo weniweni. Iwe Timoteo, usunge bwino zimene adakusungitsa. Upewe nkhani zopanda pake, zosalemekeza Mulungu, ndiponso maganizo otsutsana, amene anthu amanama kuti ndi nzeru zodziŵa zinthu. Anthu ena, chifukwa chovomereza nzeru zotere, adasokera nkutaya chikhulupiriro chao. Mulungu akukomere mtima. Ndine, Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu, mwa kufuna kwa Mulungu. Adandituma kuti ndilalike chilonjezo cha moyo umene uli mwa Khristu Yesu. Ndikulembera iwe Timoteo, mwana wanga wokondedwa. Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Ambuye athu akukomere mtima, akuchitire chifundo ndi kukupatsa mtendere. Ndikuthokoza Mulungu amene ndimamtumikira ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa, monga momwe ankachitira makolo anga. Ndimamthokoza ndikamakukumbukira kosalekeza m'mapemphero anga usana ndi usiku. Ndikamakumbukira misozi yako, ndimafunitsitsa kukuwona, kuti ndikhale ndi chimwemwe chodzaza. Ndimakumbukira chikhulupiriro chako chosanyenga. Chikhulupiriro chimenechi adaayamba ndi agogo ako aLoisi kukhala nacho. Amai ako aYunisi anali nachonso, ndipo tsopano sindikukayika konse kuti iwenso uli nacho. Nchifukwa chake ndikukukumbutsa kuti mphatso imene Mulungu adakupatsa pamene ndidakusanjika manja, uiyatsenso ngati moto. Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira. Usachite manyazi tsono kuchitira umboni Ambuye athu. Usachitenso manyazi chifukwa cha ine amene ndili m'ndende chifukwa cha iye, koma umve nao zoŵaŵa chifukwa cha Uthenga Wabwino, ndi chithandizo cha mphamvu za Mulungu. Iye adatipulumutsa, ndipo adatiitana kuti tikhale anthu ake. Sadachite zimenezi chifukwa choti ife tidaachita zabwino ai, koma chifukwa mwiniwakeyo adaazikonzeratu motero, ndiponso chifukwa mwa Khristu Yesu adatikomera mtima nthaŵi isanayambe. Koma tsopano Mulungu watiwululira zimenezi kudzera m'kuwoneka kwa Mpulumutsi wathu, Khristu Yesu. Khristuyo adathetsa mphamvu za imfa, ndipo mwa Uthenga Wabwino adaonetsera poyera moyo umene sungafe konse. Mulungu adandiika kuti ndikhale mlaliki, mtumwi ndi mphunzitsi wa Uthenga Wabwino umenewu, nchifukwa chake ndilikumva masautsoŵa. Koma sindichita manyazi, pakuti ndimamdziŵa Iye amene ndakhala ndikumkhulupirira, ndipo sindikayika kuti Iyeyo angathe kusunga bwino, mpaka tsiku la chiweruzo, zimene adandisungiza ine. Uŵagwiritse mau oona amene udamva kwa ine, kuti akhale chitsanzo choti uzitsata. Uzichita zimenezi mwa chikhulupiriro ndi mwa chikondi, zimene zili mwa Khristu Yesu. Usunge bwino zokoma zimene adakusungitsa pakutsata Mzimu Woyera amene amakhala mwa ife. Ukudziŵa kuti onse a ku dziko la Asiya adandisiya. Mwa iwowo wina ndi Figelo, wina ndi Heremogene. Ambuye achitire chifundo banja la Onesifore, chifukwa iye ankandisangulutsa kaŵirikaŵiri. Sankachita nane manyazi, ngakhale ndinali womangidwa ndi unyolo: adangoti atafika ku Roma, nkuyamba kundifunafuna mwachangu, mpaka adandipeza. Ambuye amulole kuti adzalandire chifundo kwa Mulungu pa tsiku la chiweruzo. Ukudziŵa bwino ndi iwe wemwe kuti adandithandiza kwambiri ku Efeso. Tsono iwe, mwana wanga, limbika pakugwiritsa ntchito mphatso zaulere zimene uli nazo mwa Khristu Yesu. Mau amene udamva kwa ine pamaso pa mboni zambiri, uŵasungitse anthu okhulupirika amene adzathe kuŵaphunzitsanso kwa ena. Umve nao zoŵaŵa monga msilikali wabwino wa Khristu Yesu. Msilikali amene akumenya nkhondo sasamalako ntchito zakumudzi, chifukwa iye amangofuna kukondweretsa mkulu wa ankhondo. Munthu wothamanga pa mpikisano wa liŵiro, sangalandire mphotho ngati sathamanga motsata malamulo a mpikisanowo. Mlimi wogwira ntchitoyo molimbika, ndiye ayenera kukhala woyamba kulandira nao zipatso. Uganizire bwino zimene ndikunenazi, Ambuye adzakuthandiza kumvetsa zonse. Kumbukira Yesu Khristu amene adauka kwa akufa, ndiponso anali mmodzi mwa zidzukulu za Davide, monga umaphunzitsira Uthenga Wabwino umene ine ndimalalika. Chifukwa cha Uthenga Wabwinowu ndimamva zoŵaŵa, mpakanso kumangidwa m'ndende, ngati chigaŵenga. Koma mau a Mulungu sangathe kumangidwa. Motero tsono ndimapirira zonsezi chifukwa cha anthu amene Mulungu adaŵasankha, kuti iwonso apulumutsidwe ndi Khristu Yesu, ndi kulandira ulemerero wamuyaya. Aŵa ndi mau otsimikizika ndithu: “Ngati tidafa pamodzi naye, tidzakhala moyonso pamodzi naye. Ngati tilimbika, tidzakhala mafumu pamodzi naye. Ngati ife timkana, Iyenso adzatikana. Ngati ndife osakhulupirika, Iye amakhalabe wokhulupirika, pakuti sangathe kudzitsutsa.” Uziŵakumbutsa zimenezi anthu, ndipo uŵachenjeze kolimba pamaso pa Mulungu kuti asamakangana pa za mau. Kutero kulibe phindu, koma kumangotayikitsa anthu amene akumva kukanganako. Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu, ngati wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi, wolalika mau a choona mwachilungamo. Koma nkhani zopanda pake, zosalemekeza Mulungu, uzipewe, pakuti anthu olankhula zotere adzanka nanyozeranyozera Mulungu. Ndipo zophunzitsa zao zidzaloŵerera mu anthu ngati kunyeka kwa chilonda. Mwa anthu ameneŵa wina ndi Himeneo, wina ndi Fileto. Iwowo adasokera nkusiya choona. Amaphunzitsa kuti kuuka kwa akufa kudachitika kale. Motero amasokoneza chikhulupiriro cha anthu ena. Komabe maziko olimba, amene Mulungu adaŵaika, ngokhazikika, ndipo mau olembedwapo ndi aŵa: “Ambuye amadziŵa amene ali ao”, ndiponso, “Aliyense wotamanda dzina la Ambuye, asiye zosalungama.” M'nyumba yaikulu simukhala ziŵiya zagolide kapena zasiliva zokhazokha; mumakhalanso zamtengo kapena zadothi. Zina zimakhala za ntchito zolemerera, zina za ntchito wamba. Tsono munthu akadziyeretsa nkusiya zotsikazi, adzakhala ngati chiŵiya cha ntchito zolemerera. Adzakhala wopatulika ndi wofunika zedi kwa Ambuye ake, wokonzeka kugwira ntchito iliyonse yabwino. Uthaŵe zilakolako zoipa zachinyamata. Pamodzi ndi anthu onse otama Ambuye mopemba ndi mtima woyera, uzifunafuna chilungamo, chikhulupiriro, chikondi ndi mtendere. Uzikana matsutsano opusa ndi opanda nzeru, paja ukudziŵa kuti zotere zimautsa mikangano. Ndipo mtumiki wa Ambuye asamakhala wokanganakangana ndi anthu, koma azikhala wachifundo kwa onse, mphunzitsi wokhoza, munthu wodziŵa kupirira mavuto. Akhale wofatsa polangiza otsutsana naye. Mwina Mulungu angaŵapatse mwai woti atembenuke ndi kuzindikira choona. Pamenepo nzeru zao zidzabweramo, ndipo adzapulumuka mu msampha wa Satana, amene adaaŵagwira kuti azichita zofuna zake. Udziŵe kuti pa masiku otsiriza kudzafika nthaŵi ya zovuta. Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, onyada, odzikuza, onyoza Mulungu, osamvera anakubala ao, osayamika, ndi oipitsa zinthu za Mulungu. Adzakhala opanda chifundo, osapepeseka, ndi osinjirira anzao. Adzakhala osadzigwira, aukali, odana ndi zabwino, opereka anzao kwa adani ao. Adzakhala osaopa chilichonse, odzitukumula, okonda zosangalatsa m'malo mokonda Mulungu. Adzasamala maonekedwe ake okha a chipembedzo, nkumakana mphamvu zake. Anthu otere uziŵalewa. Ena mwa iwo amaloŵa m'nyumba za anthu nkumakanyenga akazi ofooka, olemedwa ndi katundu wa machimo. Akazi ameneŵa amatengeka ndi zilakolako zamitundumitundu, amangomvera za aliyense, ndipo sangathe konse kudziŵa choona. Monga momwe Yane ndi Yambere adaaukira Mose, anthu amenewonso amaukira choona. Nzeru zao nzobuntha, ndipo pa za chikhulupiriro ndi anthu olephera. Koma sadzapitirira nazo, pakuti anthu onse adzaona kupusa kwao, monga momwe zidaachitikiranso ndi Yane uja ndi Yambere. Tsono iwe wakhala ukunditsatira m'zophunzitsa zanga, mayendedwe anga, cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa, kupirira kwanga, mazunzo anga, ndi masautso anga, monga amene adaandigwera ku Antiokeya, ku Ikonio ndi ku Listara. Ndidaazunzikadi koopsa! Koma Ambuye adandipulumutsa pa zonsezi. Onse ofuna kukhala ndi moyo wolemekeza Mulungu mwa Khristu Yesu, adzazunzikadi, m'menemo anthu ochimwa ndi onyenga, adzanka naipiraipira, ndipo azidzanyenga ena nkumanyengedwanso iwo omwe. Koma iwe, limbika pa zimene waphunzira ndipo wadziŵa kuti nzoona, paja ukuŵadziŵa amene adakuphunzitsa. Ukudziŵanso kuti kuyambira ukali mwana waŵazoloŵera Malembo Oyera, amene angathe kukupatsa nzeru zopulumukira pakukhulupirira Khristu Yesu. Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama. Motero Malembo amathandiza munthu wa Mulungu kukhala wokhoza kwenikweni, ndi wokonzekeratu kuchita ntchito yabwino iliyonse. Pamaso pa Mulungu ndi pamaso pa Khristu Yesu, amene adzaweruza anthu onse, amoyo ndi akufa omwe, ndipo potamanda kubwera kwake ndi ufumu wake wa Khristuyo ndikukulamula ndithu kuti uzilalika mau a Mulungu. Uziŵalalika molimbikira, pa nthaŵi imene anthu akuŵafuna, ngakhalenso pamene sakuŵafuna. Uziŵalozera zolakwa zao, uziŵadzudzula, uziŵalimbitsa mtima, osalephera kuŵaphunzitsa moleza mtima kwenikweni. Paja nthaŵi idzafika pamene anthu azidzakana chiphunzitso choona. M'malo mwake, chifukwa cholakalaka kumva zoŵakomera zokha, adzadzisankhira aphunzitsi ochuluka omaŵauza zimene iwo akufuna. Adzafulatira choona, osafunanso kuchimva, ndipo adzangotsata nthano chabe. Koma iwe, uzikhala maso pa zonse, pirira pa zoŵaŵa, gwira ntchito yolalika Uthenga Wabwino. Kwaniritsa udindo wako mosamala. Paja ine ndiye moyo wanga wayamba kale kuthiridwa ngati nsembe, ndipo nthaŵi yafika kuti ndinyamuke ulendo wanga wochoka m'moyo uno. Ndamenya nkhondo yabwino, ndatsiriza bwino mpikisano wa liŵiro, ndasunga chikhulupiriro. Tsopano chimene chikundidikira ndi mphotho ya chilungamo imene Mulungu wandisungira. Ambuye amene ali Woweruza wolungama, ndiwo amene adzandipatsa mphothoyo pa tsiku la chiweruzo. Tsonotu sadzangopatsa ine ndekha ai, komanso ena onse amene mwachikondi akudikira kuti Ambuyewo adzabwerenso. Uyesetse kubwera kuno msanga. Paja Dema adandisiya chifukwa chokonda zapansipano, adapita ku Tesalonika. Kresike adapita ku Galatiya, ndipo Tito adapita ku Dalamatiya. Luka yekha ndiye ali ndi ine. Ukatenge Marko udzabwere naye kuno, chifukwa amene uja angathe kundithandiza pa ntchito. Ndidatuma Tikiko ku Efeso. Pobwera unditengereko mwinjiro wanga umene ndidasiya kwa Karpo ku Troasi. Unditengerenso mabuku anga, makamaka aja azikopaŵa. Aleksandro, mmisiri wa zosulasula uja adandichita zoipa kwambiri. Ambuye adzamlanga molingana ndi zimene adachita. Iwenso uchenjere naye, chifukwa iye uja adatsutsa kwamphamvu zolalika ife. Pamene ndinkadziteteza pa mlandu wanga poyamba paja, panalibe ndi mmodzi yemwe amene adabwera kudzandithandiza, onse adangondisiya ndekha. Mulungu aŵakhululukire. Koma Ambuye adakhala nane limodzi, adandilimbitsa mtima kuti ndilalike mau onse a Uthenga Wabwino, kuti anthu a mitundu yonse aŵamve. Motero ndidapulumuka m'kamwa mwa mkango. Ambuye adzandipulumutsanso ku chilichonse chofuna kundichita choipa, ndipo adzandisunga bwino mpaka kundiloŵetsa mu Ufumu wake wa Kumwamba. Kwa Iye kukhale ulemerero kwamuyaya. Amen. Uperekeko moni kwa Prisika ndi Akwila ndiponso kwa a m'banja la Onesifore. Erasito adatsalira ku Korinto, ndipo Trofimo ndidamsiya akudwala ku Mileto. Uyesetse ndithu kubwera isanafike nyengo yachisanu. Yubulo, Pude, Lino, Klaudia, ndi abale ena onse akuti moni. Ambuye akhale nawe. Mulungu akukomereni mtima nonse. Ndine, Paulo, mtumiki wa Mulungu, ndi mtumwi wa Yesu Khristu. Adandituma kuti amene Mulungu adaŵasankha, ndiŵatsogolere ku chikhulupiriro, azizindikira choona chimene chimaŵafikitsa ku moyo wolemekeza Mulungu, ndi kuŵapatsa chiyembekezo cha moyo wosatha. Mulungu amene sanama, adalonjeza moyo wosathawu nthaŵi isanayambe. Pa nthaŵi yake Mulungu, Mpulumutsi wathu, adaululadi mau ake, ndipo adalamula kuti ine ndipatsidwe udindo wolalika uthengawu. Ndikulembera iwe Tito, mwana wanga weniweni chifukwa choti ineyo ndi iwe tili m'chikhulupiriro chimodzimodzi. Mulungu Atate ndi Khristu Yesu, Mpulumutsi wathu, akukomere mtima ndi kukupatsa mtendere. Ndidakusiya ku Krete kuti ulongosole zonse zimene zinali zisanalongosokebe, ndi kuti uike akulu a mpingo mu mzinda uliwonse, monga momwe ndidakulamulira. Mkulu wa mpingo akhale munthu wosapalamula konse, ndipo akhale wa mkazi mmodzi yekha. Ana ake akhalenso okhulupirira Khristu, opanda mbiri yoti ngosakaza kapena yoti ngosaweruzika. Woyang'anira mpingo azikhala wosapalamula konse, chifukwa ali ngati kapitao m'banja la Mulungu. Asakhale womva zayekha, kapena wopsa mtima msanga, kapena chidakwa, kapena wandeu, kapenanso wokonda kudya phindu la ndalama. Akhale wosamala bwino alendo, wokonda zabwino, wodziŵa kudzilamula, wolungama, woyera mtima, ndiponso wodzigwira. Asunge mogwiritsa mau okhulupirika, amene ali ogwirizana ndi zimene tidaphunzitsidwa. Pakutero adzatha kulimbikitsa ena ndi chiphunzitso choona, ndiponso kugonjetsa otsutsana nacho. Paja pali anthu ambiri osaweruzika, makamaka pakati pa gulu la anthu ochokera ku Chiyuda. Anthu ameneŵa amalankhula nkhani zopanda pake nkumasokeretsa anzao. Nkofunika kuŵakhalitsa chete, chifukwa akusokoneza mabanja ena athunthu pakuŵaphunzitsa zimene sayenera kuŵaphunzitsa. Amangochita zimenezi ndi cholinga choipa, chofuna kupata ndalama. Mneneri wina wa ku Krete, mmodzi mwa iwo omwewo, adati, “Akrete nthaŵi zonse ndi amabodza, zilombo zoipa, alesi adyera.” Mau ameneŵa ngotsimikizika. Nchifukwa chake uŵadzudzule kwamphamvu anthuwo, kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba, m'malo momasamala nthano zachiyuda, ndi malamulo a anthu okana choona. Kwa anthu oyera mtima, zinthu zonse nzoyera. Koma kwa amene ali odetsedwa ndi osakhulupirira, palibe kanthu koyera; mitima yao ndi nzeru zao zomwe, zonse nzodetsedwa. Amatsimikiza kuti amadziŵa Mulungu, pamene ndi zochita zao amamkana, pakuti ndi anthu onyansa osamvera, ndi osayenera kuchita kanthu kalikonse kabwino. Koma iwe uziphunzitsa zogwirizana ndi chiphunzitso choona. Uuze amuna achikulire kuti azikhala osaledzera, ochita zachiukulu, a maganizo anzeru, olimba pa chikhulupiriro, pa chikondi ndi pa kusatepatepa. Chimodzimodzinso azimai achikulire, uŵauze kuti azikhala ndi makhalidwe oyenera azimai oyera mtima. Asakhale osinjirira anzao kapena akapolo a zoledzeretsa. Akhale alangizi abwino, kuti choncho athe kuphunzitsa azimai achitsikana kukonda amuna ao ndi ana ao. Aŵaphunzitse kukhala a maganizo anzeru, opanda dama, osamala bwino zapabanja, ndi omvera amuna ao. Pamenepo anthu sanganyoze mau a Mulungu. Momwemonso amuna achinyamata uŵauzitse kuti akhale odzigwira. Pa zonse iwe wemwe ukhale chitsanzo cha ntchito zabwino. Zophunzitsa zako zikhale zoona, ndipo uziphunzitse mwaulemu. Mau ako akhale oona, kuti anthu asadzathe kuŵatsutsa. Motero wotsutsana nawe adzachita manyazi, atasoŵa kalikonse koipa kuti atinenere. Antchito azimvera ambuye ao, aziŵakondweretsa pa zonse. Asamatsutsana nawo kapena kumaŵabera, koma makamaka adziwonetse kuti ngokhulupirika pa zonse zabwino. Motero pa zochita zao zonse adzaonetsa kukoma kwake kwa zophunzitsa zonena za Mulungu, Mpulumutsi wathu. Mulungutu waonetsa kukoma mtima kwake kofuna kupulumutsa anthu onse. Kukoma mtima kwakeko kumatiphunzitsa kusiya moyo wosalemekeza Mulungu, ndiponso zilakolako za dziko lapansi. Kumatiphunzitsa kuti moyo wathu pansi pano ukhale wodziletsa, wolungama ndi wolemekeza Mulungu. Pajatu tikudikira tsiku lodala, pamene zidzachitike zimene tikuyembekeza, pamene Mulungu wamkulu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu adzaonetsa ulemerero wake. Paja Iye adadzipereka chifukwa cha ife, kuti atipulumutse ku zoipa zathu zonse, ndi kutiyeretsa kuti tikhale anthu ake achangu pa ntchito zonse zabwino. Zimenezi ndizo zimene uyenera kumaphunzitsa. Uziŵalimbikitsa anthu, ndi kuŵadzudzula komwe. Uzichita zimenezi ndi ulamuliro wonse. Wina aliyense asakupeputse ai. Uziŵakumbutsa anthu onse kuti azigonjera akulu oweruza ndi olamulira. Aziŵamvera ndipo azikhala okonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino. Uŵauze kuti asamakamba zoipa za wina aliyense, apewe kukangana, akhale ofatsa, ndipo nthaŵi zonse akhale aulemu kwa anthu onse. Pajatu kale ifenso tinali opusa, osamvera, ndi osokezedwa. Tinali akapolo a zilakolako zoipa ndi zisangalatso zamitundumitundu. Masiku onse tinkakhalira kuchita zoipa ndi kaduka, anthu kudana nafe, ndipo ife tomwe kumadana. Koma pamenepo Mulungu Mpulumutsi wathu adaonetsa kukoma kwake ndiponso chifundo chokonda anthu. Choncho adatipulumutsa osati chifukwa cha ntchito zolungama zimene ife tidaachita, koma mwa chifundo chake pakutisambitsa. Adatisambitsa mwa Mzimu Woyera pakutibadwitsa kwatsopano ndi kutipatsa moyo watsopano. Mwa Yesu Khristu, Mpulumutsi wathu, Mulungu adatipatsa Mzimu Woyerayo moolowa manja. Adachita zimenezi, kuti mwa kukoma mtima kwake tisanduke olungama pamaso pake, ndipo tikalandire moyo wosatha umene tikuuyembekeza. Ameneŵa ndi mau otsimikizika ndithu, ndipo ndikufuna kuti zimenezi unenetse, kuti okhulupirira Mulungu azidzipereka pa ntchito zabwino. Zimenezi nzabwino ndi zopindulitsa anthu. Koma upewe kufufuzafufuza zopusa, kumaŵerengaŵerenga ndondomeko za maina a makolo, mikangano, ndi mitsutso pa za Malamulo a Mose. Zimenezi nzosathandiza, zilibe phindu konse. Munthu woyambitsa mipatuko, utamdzudzula kaŵiri konse, usakhale nayenso nkanthu. Paja ukudziŵa kuti munthu wotere ngwosokonezeka ndipo ngwochimwa. Mwini wake yemwe amadziimba mlandu yekha. Ndikadzamtuma Aritema kapena Tikiko kwanuko, uchite chotheka kudzandipeza ku Nikopoli, chifukwa ndatsimikiza kuti ndikakhala kumeneko nyengo yachisanu ikubwerayi. Uyesetse kuthandiza Zena, katswiri wa malamulo uja ndiponso Apolo, kuti apitirize ulendo wao. Uwonenso kuti asasoŵe kanthu. Anthu athunso aziphunzira kudzipereka pa ntchito zabwino, kuti azithandiza pamene pali kusoŵa kwenikweni. Azitero kuti moyo wao usakhale wopanda phindu. Onse amene ali nane kuno akuti moni. Uperekeko moni kwa onse amene amatikonda chifukwa cha chikhulupiriro. Mulungu akukomereni mtima nonse. Ndine, Paulo, amene ndili m'ndende chifukwa cha Khristu Yesu. Ndili limodzi ndi Timoteo, mbale wathu. Tikulembera iwe Filemoni, bwenzi lathu ndi mnzathu wantchito. Kalata yomweyinso tikulembera Afiya, mlongo wathu, ndi Arkipo, msilikali mnzathu pa nkhondo ya Mulungu, ndiponso mpingo wonse umene umasonkhana kunyumba kwanu. Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere. Ndimayamika Mulungu wanga nthaŵi zonse ndikamakukumbukira m'mapemphero anga. Pakuti ndikumva kuti umakonda ndi kukhulupirira Ambuye Yesu, ndi oyera onse a Mulungu. Ndimapemphera kuti chikhulupiriro chimene ukugaŵana nawo chigwire ntchito mwamphamvu, kuti udziŵitsitse zabwino zonse zimene timalandira chifukwa cha Khristu. Mbale wanga, chikondi chako chandikondweretsa kwambiri ndi kundithuzitsa mtima, pakuti watsitsimutsa mitima ya oyera onse a Mulungu. Tsono, inde nkotheka kuti ndichite kukulamula m'dzina la Khristu zimene uyenera kuchita. Komabe chifukwa cha chikondi makamaka ndingochita kukupempha, ine Paulo amene ndili nkhalamba, amenenso ndili m'ndende tsopano chifukwa cha Khristu Yesu. Ndikukupempha chifukwa cha mwana wanga mwa Khristu, amene ndidachita ngati kumubala m'ndende muno. Iyeyu ndi Onesimo. Kale unalibe naye ntchito, koma tsopano angathe kutithandiza kwambiri tonsefe, iweyo ndi ine ndemwe. Ndikumtumizanso kwa iwe tsopano, ndipo pakutero ndikuchita ngati kukutumizira mtima wanga womwe. Ndikadakonda kuti akhalebe ndi ine kuno, kuti azinditumikira m'malo mwako, pokhala ndili m'ndende chifukwa cha Uthenga Wabwino. Koma sindikufuna kuchita kanthu osakufunsa, kuwopa kuti ungandichitire chinthu chabwinochi mokakamizidwa, osati mwaufulu. Kapena Onesimo adangokusiya kanthaŵi pang'ono, kuti udzakhale naye nthaŵi zonse, osatinso ngati kapolo, koma kwenikweni ngati mbale wokondedwa. Ine ndimamkonda kwambiri, ndipo iweyo uyenera kumkonda koposa, popeza kuti ndi munthu mnzako ndiponso mkhristu mnzako. Tsono ngati umati ndine bwenzi lako, umlandire iyeyu monga momwe ukadandilandirira ineyo. Ngati adakulakwirapo, kapena ali ndi ngongole kwa iwe, ngongoleyo ikhale yanga. Pano mau aŵa ndikulemba ndi dzanja langalanga kuti, “Ine Paulo ndidzalipira.” Nkosasoŵekera kukukumbutsa kuti paja iweyo ngongole yako kwa ine ndi moyo wako womwe wachikhristuwu! Tsono, mbale wanga, inenso undithandizeko chifukwa cha Ambuye. Undisangulutseko ngati mbale mwa Khristu. Ndikukulembera zimenezi, popeza kuti ndikukhulupirira kuti udzachitadi zimene ndakupempha. Ndikudziŵa kuti udzachita kopitiriranso zimene ndapemphazi. Kanthu kenanso ndi aka: undikonzere malo, chifukwa ndikhulupirira kuti Mulungu adzamvera mapemphero a inu nonse, ndi kundibwezera kwa inu. Akukupatsa moni Epafra, amene ali m'ndende pamodzi nane chifukwa cha Khristu Yesu. Akutinso moni anzanga antchito, Marko, Aristariko, Dema, ndi Luka. Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima nonse. Kale lija pa nthaŵi zosiyanasiyana, mwa njira zosiyanasiyana, Mulungu adaalankhula ndi makolo athu kudzera mwa aneneri. Koma masiku otsiriza ano walankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. Ndi mwa Iyeyu Mulungu adalenga zolengedwa zonse, namuika kuti alandire zinthu zonse ngati choloŵa chake. Iye ndiye kuŵala koonetsa ulemerero wa Mulungu, ndipo ndiye chithunzi chenicheni chosonyeza khalidwe la Mulungu. Iyeyu amachirikiza zonse ndi mau ake amphamvu. Atayeretsa mtundu wa anthu pakuŵachotsa machimo, adakakhala Kumwamba, ku dzanja lamanja la Mulungu waulemerero. Mwana wa Mulunguyo ngwoposa angelo, monga momwe dzina limene Mulungu adampatsa limaposera dzina la angelo. Nchifukwa chake nkale lonse Mulungu sadauzepo mngelo aliyense kuti, “Iwe ndiwe mwana wanga, Ine lero ndakubala.” Mulungu sadakambepo za mngelo aliyense kuti, “Ine ndidzakhala bambo wake, iye adzakhala mwana wanga.” Koma pamene ankatuma Mwana wake wachisamba pansi pano, Mulungu adati, “Angelo onse a Mulungu azimpembedza.” Ndipo za angelo Mulungu adati, “Mulungu amasandutsa angelo ake mphepo, atumiki ake amaŵasandutsa malaŵi a moto.” Koma za Mwana wake adati, “Inu Mulungu, mpando wanu wachifumu udzakhala mpaka muyaya, chilungamo ndicho chili ngati ndodo yachifumu mu ulamuliro wanu. Mudakonda chilungamo nkudana ndi zosalungama. Nchifukwa chake Ine, Mulungu wanu, ndakukwezani nkukudzozani ndi mafuta osonyeza chimwemwe, kupambana anzanu ena onse.” Adatinso, “Inu Ambuye, ndinu amene mudalenga dziko lapansi pachiyambi pomwe, zakumwambaku ndi ntchito ya manja anu. Zimenezi zidzatha, koma Inu ndinu achikhalire. Zonsezi zidzafwifwa ngati chovala. Mudzazipindapinda ngati mwinjiro, ndipo zidzasinthika ngati chovala, koma Inu ndinu osasinthika, zaka zanu sizidzatha konse.” Nkale lonse Mulungu sadauzepo mngelo aliyense kuti, “Khala ku dzanja langa lamanja mpaka ndisandutse adani ako kuti akhale ngati chopondapo mapazi ako.” Nanga angelo, kodi suja iwo ndi mizimu yotumikira chabe, imene Mulungu amaituma chifukwa cha anthu odzalandira chipulumutso? Nchifukwa chake tsono, zimene tidamva, tizizisamala kwambiri, kuwopa kuti pang'ono ndi pang'ono tingazitaye. Mau amene Mulungu adalankhula kudzera mwa angelo anali okhazikika ndithu, kotero kuti aliyense amene sadaŵamvere kapena amene adaŵanyoza, adalangidwa monga momwe kudamuyenerera. Nanga ife tingapulumuke bwanji tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotere? Ambuye ndiwo amene adalankhula poyamba za chipulumutsochi, kenaka amene adamva mau aowo, adatitsimikizira kuti ndi oona. Mulungu yemwe ankachitira umboni pakuchita zizindikiro, zinthu zozizwitsa ndi ntchito zamphamvu zamitundumitundu, ndi pakuŵagaŵira mphatso za Mzimu Woyera monga momwe Iye ankafunira. Tikamanena za dziko limene lilikudza, si angelo amene Mulungu adaŵapatsa ulamuliro pa dzikolo. Koma pena pake wina adanenetsa m'Malembo kuti, “Kodi munthu nchiyani, kuti muzimkumbukira, mwana wa munthu nchiyani, kuti muzimsamala? Kanthaŵi pang'ono mudamsandutsa wochepera kwa angelo. Mudampatsa ulemerero ndi ulemu wachifumu, ndipo mudampatsa ulamuliro pa zinthu zonse.” Tsono ngati Mulungu adapatsa munthu ulamuliro pa zinthu zonse, palibe kanthu kamene sikali mu ulamuliro wake. Komabe m'mene zinthu ziliri tsopano sitikuwona kuti zonse zakhaladi mu ulamuliro wakewo. Komatu tikuwona kuti Yesu, amene pa kanthaŵi pang'ono adaasanduka wochepera kwa angelo, adalandira mphotho ya ulemerero ndi ulemu chifukwa adamva zoŵaŵa za imfa. Zidatero chifukwa mwa kukoma mtima kwake Mulungu adaafuna kuti afere anthu onse. Paja Mulungu amene ndi Mlengi wa zonse ndipo zonse zimalinga kwa Iye, adafuna kufikitsa ana ake ambiri ku ulemerero. Tsono kudaamuyenera kuti mwa njira ya zoŵaŵa, amsandutse Yesu mtsogoleri wangwiro woŵatsogolera ku chipulumutso. Amene amayeretsa anthuyo, ndiponso anthu amene amayeretsedwawo, onse Tate wao ndi mmodzi. Nchifukwa chake Yesu sachita manyazi kuŵatchula abale ake, ponena mau akuti, “Ndidzasimbira abale anga za dzina lanu. Ndidzakutamandani pa msonkhano wa anthu anu.” Amanenanso kuti, “Ndidzakhulupirira Mulungu.” Penanso amanena kuti, “Ine ndili pano, pamodzi ndi ana amene Mulungu adandipatsa.” Tsono popeza kuti anawo ndi anthu, okhala ndi magazi ndi mnofu, Yesu yemwe adasanduka munthu wonga iwowo. Adachita zimenezi kuti ndi imfa yake aononge Satana amene anali ndi mphamvu yodzetsa imfa. Pakutero adafunanso kuti aŵamasule amene pa moyo wao wonse anali ngati akapolo chifukwa choopa imfa. Paja nchodziŵikiratu kuti sadatekeseke ndi angelo ai koma ndi zidzukulu za Abrahamu. Nchifukwa chake adaayenera kusanduka wofanafana ndi abale ake pa zonse, kuti akhale mkulu wa ansembe onse wachifundo ndi wokhulupirika potumikira Mulungu, ndipo kuti pakutero achotse machimo a anthu. Tsono popeza kuti iye yemwe adazunzikapo ndi kuyesedwapo, ndiye kuti angathe kuŵathandiza anthu amene amayesedwa. Abale, ndinu oyera ake a Mulungu, inuyo adakuitanani kuti nanunso mukhale ndi moyo wakumwamba. Nchifukwa chake muzisinkhasinkha za Yesu, mtumwi wa Mulungu, ndiponso Mkulu wa ansembe onse wa chikhulupiriro chimene timavomereza. Paja Iye anali wokhulupirika kwa Mulungu amene adampatsa udindowo, monga momwe Mosenso anali wokhulupirika m'nyumba yonse ya Mulungu. Munthu womanga nyumba amalandira ulemu woposa ulemerero wa nyumbayo. Momwemonso Yesu ngwoyenera kulandira ulemerero woposa ulemerero wa Mose. Nyumba iliyonse imamangidwa ndi munthu wakutiwakuti, koma amene adapanga zonse, ndi Mulungu. Mose anali wokhulupirika m'nyumba yonse ya Mulungu ngati wantchito chabe, kuti achitire umboni zimene Mulungu analikudzanena m'tsogolo mwake. Koma Khristu anali wokhulupirika m'nyumba ya Mulungu ngati mwana wolamulira pa zonse za m'nyumba mwakemo. Ndipo nyumba yakeyo ndife, ngati tiika mphamvu pa kulimba mtima ndi kunyadira zimene tikuziyembekeza. Nchifukwa chake tsono, monga Mzimu Woyera akunenera, “Lero lino mukamva mau a Mulungu, musaumitse mitima yanu monga muja zidaachitikira pomuukira Mulungu, tsiku la kumuyesa m'chipululu muja. Mulungu akuti, Pamene paja, makolo anu adaandiputa pakundiyesa, ndipo adaona zimene ndidaŵachita pa zaka makumi anai. Tsono ndidaukwiyira mbadwowo, ndipo ndidati, ‘Nthaŵi zonse amasokera mumtima mwao, sanaphunzirebe njira zanga.’ Motero ndili wokwiya ndidalumbira kuti, ‘Sadzaloŵa konse mu mpumulo umene ndidaŵakonzera.’ ” Abale, mchenjere, kuti pasapezeke wina aliyense mwa inu wokhala ndi mtima woipa ndi wosakhulupirira, womlekanitsa ndi Mulungu wamoyo. Kwenikweni muzilimbikitsana tsiku ndi tsiku ikadalipo nthaŵi, imene m'mau a Mulungu imatchedwa kuti, “Lero”. Muzichita zimenezi, kuwopa kuti wina aliyense mwa inu angaumitsidwe mtima ndi chinyengo cha uchimo. Paja timasanduka anzake a Khristu, malinga tikasunga kwenikweni mpaka potsiriza kulimba mtima kumene tinali nako poyamba. Paja Malembo akuti, “Lero lino mukamva mau a Mulungu, musaumitse mitima yanu monga muja zidaachitikira poukira Mulungu.” Nanga amene adaamva mau ake a Mulungu namuukira, ndani? Ndi onse aja amene Mose adaaŵatsogolera nkuŵatulutsa m'dziko la Ejipito. Nanga amene Mulungu adaaŵakwiyira zaka makumi anai, ndani? Ndi anthu amene adaachimwa aja, mitembo yao nkutsalira m'chipululu. Nanga Mulungu ankanena za yani pamene adaati, “Ndikulumbira kuti ameneŵa sadzaloŵa konse mu mpumulo umene ndidaŵakonzera?” Pajatu ankanena za anthu amene adaamuukira. Motero tikuwona kuti anthuwo sadathe kuloŵa, chifukwa cha kusakhulupirira. Lonjezo la Mulungu lakuti tidzaloŵa mu mpumulo umene Iye adatikonzera, lilipobe. Tsono tichenjere kuti pasakhale wina aliyense mwa inu wopezeka kuti walephera kuloŵamo. Paja ifenso tidaumva Uthenga Wabwino, monga iwo aja. Koma iwowo sadapindule nawo mau olalikidwawo, popeza kuti adangoŵamva, koma osaŵakhulupirira. Ife okhulupirirafe tikuloŵamo mu mpumulowo. Paja Mulungu adaanena kuti, “Ndili wokwiya ndidalumbira kuti, ‘Sadzaloŵa konse mu mpumulo umene ndidaŵakonzera.’ ” Adaanena zimenezi, ngakhale anali atatsiriza ntchito zake zonse za kulenga dziko lapansi. Pena pake ponena za tsiku lachisanu ndi chiŵiri pali mau akuti, “Mulungu adapumula pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri, kuleka ntchito zake zonse.” Panonso akunena za zomwezo pamene akuti, “Sadzaloŵa konse mu mpumulo umene ndidaŵakonzera.” Mulungu adakonza kuti ena aloŵe ndithu mu mpumulowo, koma aja adaamva Uthenga Wabwino poyambaŵa sadaloŵemo chifukwa cha kusamvera. Nchifukwa chake Mulungu adaikanso tsiku lina, lotchedwa kuti “Lero”. Patapita nthaŵi yaitali Mulungu adalankhula za tsiku lomweli kudzera mwa Davide ponena mau aja tatchula kaleŵa, akuti, “Lero, mukamva mau a Mulungu, musaumitse mitima yanu.” Chifukwatu Yoswa akadaŵaloŵetsa anthuwo mu mpumulo uja, sibwenzi pambuyo pake atanena za tsiku linanso. Nchifukwa chake tsono mpumulo wonga wa pa Sabata waŵatsalirabe anthu a Mulungu. Paja munthu woloŵa mu mpumulo umene Mulungu adalonjeza, nayenso amapumula, kuleka ntchito zake, monga momwe Mulungu adaapumulira, kuleka ntchito zake. Tiyesetse tsono kuloŵa mu mpumulowo, kuwopa kuti wina aliyense angakhale wosamvera monga iwo aja, nalephera kuloŵamo. Paja mau a Mulungu ndi amoyo ndi ogwira ntchito mwamphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amabaya mpaka molumikizirana mwa moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana mfundo ndi mafuta a m'mafupa. Amaweruza ngakhale zimene anthu amalingalira ndi kulakalaka m'mitima mwao. Pamaso pa Mulungu palibe kanthu kobisika, zonse zili poyera ndipo nzovundukuka pamaso pa Iye amene tiyenera kumufotokozera zonse zimene tachita. Tiyeni tsono, tigwiritse chikhulupiriro chimene timavomereza. Pakuti tili naye Mkulu wa ansembe wopambana, amene adapita mpaka kukafika kumwamba kwenikweni kwa Mulungu. Iyeyu ndi Yesu, Mwana wa Mulungu. Sitili ndi Mkulu wa ansembe woti sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofooka zathu. Wathu Mkulu wa ansembe onse adayesedwa pa zonse, monga momwe ife timayesedwera, koma Iye sadachimwe konse. Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni. Mkulu wa ansembe aliyense amasankhidwa pakati pa anthu, namuika kuti aziŵaimirira pamaso pa Mulungu. Ntchito yake nkupereka mphatso ndi nsembe chifukwa cha machimo. Popeza kuti iye yemweyo ali ndi zofooka zambiri, ndiye kuti angathe kuŵalezera mtima amene ali opanda nzeru ndi osokera. Nchifukwa chake aumirizidwa kumapereka nsembe chifukwa cha machimo a iye yemwe, ndiponso machimo a anthu ena. Palibe munthu amadzitengera yekha ulemu wokhala mkulu wa ansembe onse, koma amachita kuitanidwa ndi Mulungu, monga momwe adaaitanidwira Aroni. Momwemonso Khristu sadadzikweze yekha ku ulemu wokhala mkulu wa ansembe onse, koma Mulungu ndiye adachita kumuuza kuti, “Iwe ndiwe Mwana wanga, Ine lero ndakubala.” Penanso Mulungu adati, “Ndiwe wansembe mpaka muyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.” Yesu, pa nthaŵi imene anali munthu pansi pano, mofuula ndi molira misozi, adapereka mapemphero ndi madandaulo kwa Mulungu, amene anali nazo mphamvu zompulumutsa ku imfa. Ndiye popeza kuti Yesu adaadzipereka modzichepetsa, Mulungu adamvera mapemphero ake. Motero Yesu, ngakhale anali Mwana wa Mulungu, adaphunzira kumvera pakumva zoŵaŵa. Atasanduka wangwiro kotheratu, adakhala gwero la chipulumutso chosatha kwa onse omvera Iye, ndipo Mulungu adamtchula mkulu wa ansembe onse, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki. Tili ndi zambiri zoti nkunena pa zimenezi, koma nzovuta kufotokoza kwake, popeza kuti mwasanduka ouma mitu. Lija nkale mukadayenera kukhala ophunzitsa anzanu, komabe nkofunika kuti wina akuphunzitseninso maphunziro oyamba enieni a mau a Mulungu. Nkofunikanso kukumwetsani mkaka, m'malo mwa kukupatsani chakudya cholimba. Ngati wina aliyense angomwa mkaka, ndiye kuti akali mwana wakhanda, sangathe kutsata chiphunzitso chofotokoza za chilungamo. Koma chakudya cholimba ndi cha anthu okhwima. Pakugwiritsa ntchito nzeru zao, iwoŵa adadzizoloŵeza kusiyanitsa pakati pa zabwino ndi zoipa. Tsono tisangoima pa maphunziro oyamba enieni a Khristu. Tisachite kubwerezanso kuphunzitsa zomwe zili ngati maziko, monga za kutembenuka mtima kusiya ntchito zosapindulitsa moyo wosatha, za kukhulupirira Mulungu, za maubatizo, za kusanjika manja, za kuuka kwa akufa, ndi za chiweruzo chotsiriza. Koma tiyeni tipitirire mpaka tikafike pa kukhwima kwenikweni. Mulungu akalola, tidzaterodi. Anthu amene adataya chikhulupiriro chao, nkosatheka kuŵatsitsimutsa kuti atembenuke mtima. Iwowo kale Mulungu adaaŵaunikira, adaalaŵako mphatso yochokera Kumwamba, nkulandira nao Mzimu Woyera. Ndipo adazindikira kukoma kwa mau a Mulungu, ndi mphamvu za nthaŵi imene inalikudzafika. Tsono akamkana Mulungu tsopano, akuchita ngati kumpachika iwo omwe Mwana wa Mulungu, ndi kumnyozetsa poyera. Paja nthaka yolandira mvula kaŵirikaŵiri, nkubereka mbeu zopindulitsa oilima, Mulungu amaidalitsa. Koma ngati ibereka minga ndi nthula, ndi yachabe ndipo ili pafupi kutembereredwa. Mathero ake nkutenthedwa m'moto. Koma inu okondedwa anga, ngakhale tikunena zimenezi, sitikukukayikirani. Tikudziŵa kuti muli nazo zabwino, zolinga ku chipulumutso chanu. Paja Mulungu ngwolungama, sangaleke kusamalako za ntchito zanu, ndi chikondi chimene mudaamuwonetsa pakutumikira oyera ake, monga m'mene mukuchitirabe tsopano. Tikufunitsitsa kuti aliyense mwa inu apitirire kuwonetsa changu chomwechi mpaka potsiriza, kuti chiyembekezo chanu chifike pake penipeni. Sitifuna kuti mukhale aulesi, koma kuti mutsanzire anthu amene, pakukhulupirira ndi pakupirira, akulandira zimene Mulungu adalonjeza. Pamene Mulungu ankamulonjeza kanthu Abrahamu, adaalumbira kuti, “Pali Ine ndemwe, Mulungune.” Adaatero, popeza kuti panalibe wamkulu koposa Mwiniwakeyo amene akadamtchula polumbirapo. Ndiye Mulungu adati, “Ndithudi ndidzakudalitsa kwakukulu, ndipo ndidzachulukitsa kwambiri zidzukulu zako.” Nchifukwa chake Abrahamu adaayembekeza molimbikira, nalandira zimene Mulungu adaamlonjeza. Anthu amalumbira m'dzina la wina amene akuŵaposa, ndipo lumbiro lotere lotsimikizira mau, limathetsa kutsutsana konse pakati pao. Mulungu pofuna kuŵatsimikizira anthu odzalandira zimene adaalonjeza, kuti Iye sangasinthe maganizo, adatsimikiza lonjezo lakelo pakulumbira. Motero pali zinthu ziŵirizi, lonjezo ndi lumbiro, zimene sizingathe kusinthika, ndipo Mulungu sanganamirepo. Mwa zimenezi Mulungu adafuna kutilimbitsa mtima ife amene tidathaŵira kwa Iye, kuti tichigwiritse chiyembekezo chimene adatiikira pamaso pathu. Chiyembekezo chimenechi tili nacho ngati nangula wa moyo wathu. Nchokhazikika, nchosagwedezeka konse, ndipo chimabzola chochinga cha Nyumba ya Mulungu ya Kumwamba, nkukaloŵa mpaka ku Malo Opatulika am'katikati. Yesu adatitsogolera kale nkuloŵamo chifukwa cha ife. Iye adasanduka mkulu wa ansembe onse wamuyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki. Melkizedeki ameneyu anali mfumu ya ku Salemu, ndiponso wansembe wa Mulungu Wopambanazonse. Pamene Abrahamu ankabwerako kuchokera ku nkhondo, atagonjetsa mafumu aja, Melkizedeki adadzamchingamira, namdalitsa. Abrahamu adampatsa chigawo chachikhumi cha zonse zimene adaafunkha. Potsata tanthauzo la dzina lake, choyamba Melkizedeki ndi “Mfumu ya chilungamo,” pambuyo pake ndi “Mfumunso ya Salemu,” ndiye kuti, “Mfumu ya Mtendere”. Za bambo wake kapena mai wake, kapena makolo ake, palibe chilichonse chidalembedwa. Chimodzimodzi za kubadwa kwake ndi imfa yakenso. Ali ngati Mwana wa Mulungu, akupitiriza kukhala wansembe mpaka muyaya. Mukuwonatu tsono kuti munthuyo anali wamkulu ndithu. Nanga Abrahamu, kholo lathu lija, kuchita kumpatsa chachikhumi cha zimene adaafunkha! Malamulo a Mose amati ana a Levi, amene ali ansembe, azilandira chachikhumi kwa Aisraele. Ndiye kuti iwo amalandira kwa abale ao, ngakhale abalewo nawonso ndi ana a Abrahamu. Melkizedeki sanali m'gulu la zidzukulu za Levi, komabe adalandira chachikhumi kwa Abrahamu. Ndipo adadalitsa Abrahamu, munthu amene anali atalandira malonjezo a Mulungu. Paja nchodziŵikiratu kuti munthu wodalitsa mnzake ndiye wamkulu kuposa amene akudalitsidwayo. Kunena za ansembe olandira chachikhumi aja, amene ndi zidzukulu za Levi, iwoŵa ndi anthu otha kufa. Koma kunena za Melkizedeki, Malembo amamchitira umboni kuti ngwamoyo. Kwenikweni tingathe kunena kuti pamene Abrahamu ankapereka chachikhumi, Levi yemwe, amene amalandira chachikhumi, adaapereka nao chachikhumicho. Pakuti iye anali akadali m'thupi la kholo lake Abrahamu pamene Melkizedeki adadzamchingamira. Malamulo amene Aisraele adalandira, anali okhazikika pa unsembe wa Levi. Tsono achikhala kudaali kotheka kukhala angwiro mwa unsembe umenewu, sikukadafunikanso unsembe wina, wonga uja wa Melkizedeki, wosiyana ndi wonga uja wa Aroni. Pakuti pakakhala kusintha pa unsembe, ndiye kuti pa Malamulonso sipangalephere kukhala kusintha. Ambuye athu, amene mauŵa akunena za Iwo, anali a fuko lina. Ndipo palibiretu wa fuko limeneli amene adatumikirapo ku guwa lansembe. Nchodziŵikiratu kuti Ambuye athu aja anali a fuko la Yuda, ndipo Mose pokamba za fuko limeneli, sadanenepo kanthu za ansembe. Nkhaniyi imamveka bwino koposa pamene tiwona kuti pafika wansembe wina wonga Melkizedeki. Iyeyo sadakhale wansembe chifukwa cha malamulo okhudza kubadwa kwa anthu, koma chifukwa cha mphamvu za moyo wake umene uli wosatha. Paja mau a Mulungu pomuchitira umboni akuti, “Ndiwe wansembe mpaka muyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.” Motero lamulo lakale lalekeka chifukwa linali lopanda mphamvu, linali lopanda phindu. Pajatu Malamulo a Mose sankatha kusandutsa munthu kuti akhale wangwiro. Koma m'malo mwake mwaloŵa chiyembekezo choposa, ndipo mwa chiyembekezo chimenechi timayandikira kwa Mulungu. Chinanso nchakuti Mulungu adaachita kulumbira. Amene ankaloŵa unsembe kale lija ankatenga udindo waowo popanda lumbiro. Koma Yesu adaloŵa unsembe wake ndi lumbiro, pamene Mulungu adamuuza kuti, “Ambuye adalumbira, ndipo sadzasintha maganizo ake akuti, ndiwe wansembe mpaka muyaya.” Kusiyana kokhudza lumbiroku kukutiwonetsa kuti Yesu ndi Nkhoswe yotsimikizira Chipangano choposa. Kusiyana kwina nkwakuti ansembe akale aja anali ambiri, chifukwa ankafa, sankatha kupitirira ndi udindo waowo. Koma Yesu ngwamuyaya, motero unsembe wake ngwosasinthika. Nchifukwa chake angathe kuŵapulumutsa kwathunthu anthu amene akuyandikira kwa Mulungu kudzera mwa Iye, pakuti Iyeyo ali ndi moyo nthaŵi zonse kuti aziŵapempherera. Tsono padaafunika kuti tikhale naye wotere mkulu wa ansembe onse: woyera mtima, wopanda choipa kapena chodetsa chilichonse, wosiyana ndi anthu ochimwa, ndiponso wokwezedwa kubzola zonse zakumwambaku. Yesu ameneyu sali ngati akulu a ansembe ena aja. Palibe chifukwa chakuti tsiku ndi tsiku azipereka nsembe poyamba chifukwa cha machimo ake, kenaka chifukwa cha machimo a anthu. Zimenezi adachitiratu kamodzi kokha, pakudzipereka yekha ngati nsembe. Malamulo a Mose amaika anthu amene ali ndi zofooka, kuti akhale akulu a ansembe onse. Koma mau a lumbiro la Mulungu lija limene lidabwera pambuyo pa Malamulowo, adaika Mwana wake, amene wakhala wangwiro kwamuyaya kuti akhale mkulu wa ansembe onse. Mfundo yeniyeni pa zimene tikunenazi ndi iyi: tili naye wotere Mkulu wa ansembe onse, amene akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu Waulemerero Kumwamba. Iye akutumikira m'Malo Opatulika am'katikati, ndiye kuti m'chihema chenicheni chimene adachimanga ndi Ambuye osati munthu ai. Paja mkulu wa ansembe aliyense amaikidwa kuti azipereka mphatso ndi nsembe kwa Mulungu. Motero nkofunika kuti wathunso mkulu wa ansembe onse akhale nkanthu koti apereke. Iyeyu akadakhala pa dziko lapansi, sibwenzi ali wansembe konse, popeza kuti alipo kale ansembe amene amapereka mphatso potsata Malamulo a Mose. Ntchito za chipembedzo zimene iwo amachita, zili ngati chithunzi chongofanizira zenizeni za Kumwamba. Paja zidaateronso ndi Mose: pamene iye adaati amange chihema, Mulungu adaamlangiza kuti, “Upangetu zonse molingana ndi chitsanzo chimene ndidaakuwonetsa paphiri paja.” Koma monga zilirimu, Yesu adalandira unsembe wopambana kutalitali unsembe wakale uja, monga momwe ndiyenso Nkhoswe ya chipangano chopambana, chifukwa malonjezo ake ngopambana malonjezo a chipangano chakale chija. Chipangano choyamba chija chikadakhala changwiro, sipakadafunikanso china m'malo mwake. Koma Mulungu adadzudzula anthu ake ndi mau aŵa akuti, “Masiku akubwera, pamene ndidzachita chipangano chatsopano ndi fuko la Israele, ndiponso ndi fuko la Yuda. Sichidzakhala chonga chipangano chimene ndidaachita ndi makolo ao tsiku limene ndidaachita kuŵagwira pa dzanja kuti ndiŵatulutse m'dziko la Ejipito. Chifukwa iwo sadasunge chipangano changa chija, nanenso sindidaŵasamale”, akutero Ambuye. “Nachi tsono chipangano chimene ndidzachita ndi fuko la Israele atapita masiku ameneŵa,” akutero Ambuye: “Ndidzaika Malamulo anga m'maganizo ao ndidzachita kuŵalemba m'mitima mwao. Choncho Ine ndidzakhala Mulungu wao, iwowo adzakhala anthu anga. Sipadzafunikanso kuti wina aliyense aphunzitse mnzake, kapena kuti wina aliyense auze mbale wake kuti, ‘Udziŵe Ambuye’. Pakuti onse adzandidziŵa, kuyambira wamng'ono mpaka wamkulu. Mwachifundo ndidzaŵakhululukira zochimwa zao, sindidzakumbukiranso machimo ao.” Pakunena mau oti, “Chipangano chatsopano”. Mulungu akunena kuti chipangano choyamba nchotha ntchito. Paja chinthu chimene chayamba kutha ntchito nkumakalamba, ndiye kuti chili pafupi kuzimirira. Chipangano choyamba chija chinali nawo malamulo okhudza chipembedzo, chinalinso ndi malo opembedzeramo omangidwa ndi anthu. Anthu adaamanga chihema, ndipo m'chipinda chake choyamba munkakhala choikaponyale, tebulo, ndi mikate yoperekedwa kwa Mulungu. Chipinda chimenechi chinkatchedwa “Malo Opatulika.” Paseri pa chochinga chachiŵiri panali chipinda chotchedwa “Malo Opatulika Kopambana”. Chipindachi chinali ndi guwa lagolide lofukizirapo lubani. M'chipindamo munalinso bokosi lachipangano. Bokosi lonselo linali lokutidwa ndi golide. M'bokosimo munali kambiya kagolide m'mene munali mana uja, ndi ndodo ya Aroni, ija idaaphukayi. Munalinso miyala iŵiri ija yolembedwapo mau a chipangano. Pamwamba pa bokosilo panali zithunzi za akerubi oonetsa ulemerero wa Mulungu. Mapiko ao adaaphimbira pa chivundikiro cha bokosilo chimene chinali malo okhululukirapo machimo. Koma nkosatheka tsopano lino kufotokoza zonzezi tsatanetsatane. Malinga ndi malongosoledwe ameneŵa, ansembe amaloŵa m'chipinda choyamba chija masiku onse pokagwira ntchito zao za chipembedzo. Koma m'chipinda chachiŵiri chija ndi mkulu wa ansembe onse yekha amene amaloŵamo, nayenso ndi kamodzi kokha pa chaka, ndipo saloŵamo popanda kutenga magazi. Magaziwo ngokapereka kwa Mulungu chifukwa cha iye mwini, ndiponso chifukwa cha machimo ochita anthu mosazindikira bwino. Mwa njira imeneyi Mzimu Woyera akuphunzitsa kuti njira yoloŵera m'Malo Opatulika Kopambana ndi yosatsekukabe pamene chipinda choyamba chija chilipobe. Zimenezi nzofanizira chabe, ndipo zimaloza ku nthaŵi ino. Potsata malongosoledwe ameneŵa mphatso ndi nsembe zimene munthu amapereka sizingathe konse kuusandutsa wangwiro mtima wa wopembedzayo. Zimangonena za zakudya, za zakumwa, ndi za miyambo yosiyanasiyana ya kasambidwe. Zonsezo ndi malamulo olinga pa zooneka ndi maso chabe, oikidwa kuti azingokhalapo mpaka nthaŵi imene Mulungu adzakonzenso zonse. Koma Khristu wafika, ndipo ndiye Mkulu wa ansembe onse wa zokoma zimene zilikudza tsopano. Chihema chimene Iye amatumikiramo nchachikulu ndiponso changwiro kopambana. Nchosapangidwa ndi anthu, ndiye kuti si chapansipano. Pamene Khristu adabzola chihemachi, nkukaloŵa kamodzi kokhako m'malo Opatulika Kopambana, sadaloŵemo ndi magazi a atonde ndi a anaang'ombe amphongo ai. Adaloŵamo ndi magazi akeake. Potero adatikonzera chipulumutso chosatha. Magazi a atonde ndi a ng'ombe zamphongo, ndiponso phulusa la mwanawang'ombe wamkazi zimawazidwa pa anthu amene ali odetsedwa chifukwa chosasamala mwambo wachiyuda. Zimenezi zimaŵayeretsa pakuŵachotsa litsiro lam'thupi. Nanji tsono magazi a Khristu, angathe kuchita zoposa. Mwa Mzimu wamuyaya Iye adadzipereka ngati nsembe yopanda chilema kwa Mulungu. Ndiye kuti magazi ake adzayeretsa mitima yathu pakuichotsera ntchito zosapindulitsa moyo, kuti tizitumikira Mulungu wamoyo. Nchifukwa chake Khristu ndi Nkhoswe ya chipangano chatsopano, kuti amene Mulungu adaŵaitana, alandire madalitso osatha amene Mulunguyo adalonjeza. Izi zidatheka chifukwa cha imfa ya Khristu, imene imapulumutsa anthu ku zochimwa zozichita akali m'Chipangano choyamba chija. Ngati munthu alemba Chipangano chosiyira ena chuma, pafunika kutsimikiza kuti wolemba chipanganocho wamwaliradi. Paja chipangano chotere chilibe mphamvu, asanamwalire wochilemba. Chimakhala ndi mphamvu pokhapokha wochilembayo atamwalira. Nchifukwa chake ngakhale Chipangano choyamba chija sichidachitike popanda kukhetsa magazi. Poyamba Mose adaalengeza kwa Aisraele malamulo onse, motsata Malamulo amene Mulungu adaampatsa. Pambuyo pake adatenga magazi a anaang'ombe amphongo ndi madzi, nawaza pa buku la Malamulo ndi pa anthu onse. Adaachita zimenezi ndi kanthambi ka chitsamba cha hisope, ndiponso ndi ubweya wankhosa wofiira. Pochita zimenezi adanenerera mau akuti, “Aŵa ndi magazi otsimikizira Chipangano chimene Mulungu walamula kuti mchisunge.” Momwemonso Mose adawaza magazi pa chihema ndi pa ziŵiya zonse zogwirira ntchito pa chipembedzo. Malinga ndi Malamulo a Mosewo pafupifupi zonse zimayeretsedwa ndi magazi, ndipo machimo sakhululukidwa popanda kukhetsa magazi. Tsono padaafunika kuti zinthu zongofanizira zenizeni za Kumwamba, ziyeretsedwe ndi miyambo imeneyi. Koma kuti za Kumwamba zenizenizo ziyeretsedwe, padaafunika nsembe zina zoposa zimenezo. Paja Khristu sadaloŵe m'malo opatulika omangidwa ndi anthu, malo ongofanizira malo enieni opatulika a Kumwamba. Iye adapita Kumwamba kwenikweniko, kuti tsopano aziwonekera pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife. Mkulu wa ansembe onse amaloŵa m'Malo Opatulika Kopambana chaka ndi chaka atatenga magazi amene sali ake. Koma Khristu sadaloŵe Kumwamba kuti azidzipereka nsembe kaŵirikaŵiri. Zikadatero, akadayenera kumamva zoŵaŵa kaŵirikaŵiri chilengedwere cha dziko lapansi. Koma monga zilirimu, waoneka kamodzi kokha pakutha pake pa nthaŵi yotsiriza, kuti achotse uchimo pakudzipereka yekha nsembe. Munthu aliyense amafa kamodzi kokha, pambuyo pake nkumaweruzidwa. Momwemonso Khristu adaperekedwa nsembe kamodzi kokha, kuti asenze ndi kuchotsa machimo a anthu ambiri. Adzaonekanso kachiŵiri, osati kuti adzachotsenso uchimo ai, koma kuti adzapulumutse anthu amene akumuyembekeza. Malamulo a Mose ndi chithunzi chabe cha madalitso amene alikudza, osati madalitso enieniwo. Ngakhale nsembe zimodzimodzi zimaperekedwa kosalekeza chaka ndi chaka, Malamulowo sangathe konse mwa nsembezo kuŵasandutsa angwiro anthu oyandikira pamenepo. Anthu opembedza Mulungu aja akadayeretsedwa kwathunthu, sibwenzi mtima wao ukuŵatsutsabe, ndipo akadaleka kumapereka nsembe. Koma monga zilirimu, nsembezo zimakumbutsa anthu za machimo ao chaka ndi chaka. Magazi a ng'ombe zamphongo ndi a atonde sangathe konse kuchotsa machimo. Nchifukwa chake pamene Khristu adadza pansi pano, adati, “Inu Mulungu simudafune nsembe kapena zopereka, koma thupi mudandikonzera. Nsembe zoocha kwathunthu ndi nsembe zoperekera machimo, simudakondwere nazo. Tsono ine ndidati, ‘Inu Mulungu, ndabweratu kuti ndichite zimene mukufuna, paja zidalembedwa choncho ponena za Ine m'buku la Malamulo.’ ” Motero poyamba adati, “Nsembe kapena zopereka, nsembe zopsereza kwathunthu kapenanso nsembe zoperekera machimo, simudazifune ndipo simudakondwere nazo.” Zimenezi nzimene Malamulo adaanena kuti ziperekedwe. Koma pambuyo pake adati, “Ndabweratu, kuti ndichite zimene mukufuna.” Motero Khristu adathetsa mphamvu za nsembe za mtundu woyamba zija, kuti m'malo mwake akhazikitse nsembe ya mtundu wachiŵiriyo. Chifukwa chakuti Yesu Khristu adachita zimene Mulungu adaafuna kuti achite, ife tidayeretsedwa ndi nsembe ya thupi lake, limene Iye adapereka kamodzi kokhako. Wansembe aliyense amaimirira tsiku ndi tsiku nkumatumikira, ndipo amapereka nsembe imodzimodzi mobwerezabwereza. Komabe nsembe zimenezi sizingathe konse kuchotsa machimo. Koma Khristu adapereka nsembe imodzi yokha yochotsera machimo onse. Ndipo ataipereka, adakakhala ku dzanja lamanja la Mulungu. Kumeneko akudikira tsono kuti Mulungu asandutse adani ake kukhala ngati chopondapo mapazi ake. Mwa nsembe imodzi yomweyo wasandutsa angwiro kwamuyaya onse amene Iye akuŵayeretsa. Mzimu Woyera nayenso amatitsimikizira zimenezi. Poyamba Iye akuti, “Nachi chipangano chimene ndidzachita nawo atapita masiku amenewo, akutero Ambuye: ndidzaika Malamulo anga m'mitima mwao, ndidzachita kuŵalemba m'maganizo ao.” Pambuyo pake akutinso, “Sindidzaŵakumbukiranso konse machimo ao ndi zolakwa zao.” Pamene Mulungu wakhululukira zonsezi, sipafunikanso nsembe yoperekera machimo. Motero tsono, abale, timayembekeza mosakayika konse kuloŵa m'Malo Opatulika Kopambana chifukwa cha imfa ya Yesu. Iye adatitsekulira njira yatsopano ndi yamoyo yobzola chochinga, chimene chili thupi lake. Ndiponso tili ndi Wansembe wamkulu woyang'anira nyumba ya Mulungu. Nchifukwa chake tsono, tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona, tili ndi chitsimikizo cha chikhulupiriro. Timuyandikire ndi mitima yoyeretsedwa, yopanda kalikonse koitsutsa, ndiponso ndi matupi osambitsidwa ndi madzi oyera. Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika. Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira. Pakuti tikamachimwirachimwira mwadala, kwina tikudziŵa choona, palibenso nsembe ina iliyonse ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo. Pamenepo chotitsalira si china ai, koma kumangodikira ndi mantha chiweruzo, ndiponso moto woopsa umene udzaononga otsutsana ndi Mulungu. Munthu wophwanya Malamulo a Mose amaphedwa popanda nchifundo chomwe, malinga pakakhala mboni ziŵiri kapena zitatu. Nanji tsono munthu wonyoza Mwana wa Mulungu, munthu woyesa chinthu chachabe magazi achipangano amene adamuyeretsa, munthu wonyoza Mzimu wotipatsa madalitso a Mulungu! Chilango cha munthu wotere chidzakhala choopsa kopambana. Paja tikumdziŵa kale amene adati, “Kulipsira nkwanga, ndidzakhaulitsa ndine.” Adatinso, “Ambuye adzaweruza anthu ake.” Kugwa m'manja mwa Mulungu wamoyo ndi chinthu choopsa. Kumbukirani masiku akale aja mutangolandira kuŵala chatsopano. Pa nthaŵi imene ija mudaalimbana ndi mazunzo ambiri. Mwina ankakunyozani ndi kukuchitani chipongwe, anthu akuwonerera. Mwinanso munkamva nawo zoŵaŵa amene ankasautsidwa motero. Munkasaukira limodzi ndi amene adaaponyedwa m'ndende, ndipo mudalola mokondwa kuti alande chuma chanu, mutadziŵa kuti muli ndi chuma choposa ndi chosatha. Tsono musataye kulimba mtima kwanu, pakuti kumabweretsa mphotho yaikulu. Pafunikadi kupirira, kuti muchite zimene Mulungu akufuna, kuti motero mukalandire zimene adalonjeza. Paja Malembo akuti, “Pangotsala kanthaŵi pang'ono chabe kuti Iye amene alikudza, afike. Sachedwa ai. Wolungama wanga adzakhala ndi moyo pakukhulupirira. Koma akamachita mantha nkubwerera m'mbuyo, Ine sindikondwera naye.” Ifetu sindife anthu oti nkumabwerera m'mbuyo ndi kutayika ai, ndife anthu okhulupirira, kuti tipulumuke. Tikati kukhulupirira, ndiye kuti kusakayika konse pa zinthu zimene tikuziyembekeza, ndiponso kutsimikiza kuti zinthu zimene sitikuziwona zilipo ndithu. Pokhala ndi chikhulupiriro, makolo anthu akale aja Mulungu adaonetsa kuti ankakondwera nawo. Pokhala ndi chikhulupiriro timamvetsa kuti zonse zimene zilipo zidalengedwa ndi mau a Mulungu, mwakuti zinthu zoonekazi zidachokera ku zinthu zosaoneka. Pokhala ndi chikhulupiriro, Abele adapereka kwa Mulungu nsembe yopambana ya Kaini, navomerezedwa kuti ngwolungama, chifukwa Mulungu mwiniwake adaamchitira umboni pakulandira zopereka zake. Mwakuti ngakhale iye adafa, koma chifukwa cha chikhulupiriro chakecho, akulankhulabe mpaka pano. Pokhala ndi chikhulupiriro, Enoki adatengedwa kupita Kumwamba, osafa konse. Sadapezekenso, popeza kuti Mulungu adamtenga. Malembo amamchitira umboni kuti asanatengedwe, anali wokondweretsa Mulungu. Ndipotu popanda chikhulupiriro nkosatheka kukondweretsa Mulungu. Paja aliyense wofuna kuyandikira kwa Mulungu, ayenera kukhulupirira kuti Mulunguyo alipodi, ndipo kuti amaŵapatsa mphotho anthu omufunafuna. Pokhala ndi chikhulupiriro, Nowa adalandira machenjezo a Mulungu onena za zinthu zomwe mpaka nthaŵi imeneyo zinali zisanaoneke. Adamvera, napanga chombo kuti apulumutse onse a m'banja mwake. Potero adaŵatsutsa kuti ngolakwa anthu a dziko lapansi, nalandira chilungamo chimene Mulungu amapatsa anthu omkhulupirira. Pokhala ndi chikhulupiriro, Abrahamu adamvera pamene Mulungu adamuitana kuti apite ku dziko lina limene adaamlonjeza kuti lidzakhala lake. Ngakhale sankadziŵa kumene ankapita, adapitabe. Pokhala ndi chikhulupiriro chomwecho, ankakhala ngati mlendo m'dzikolo limene Mulungu adaamlonjeza. Ankakhala m'mahema pamodzi ndi Isaki ndi Yakobe, amene nawonso anali atalandira lonjezo lomwelo la Mulungu. Monsemo Abrahamu ankadikira mzinda wa maziko okhazikika. Mzindawo, Mmisiri woganiziratu mamangidwe ake ndiponso woumanga, ndi Mulungu. Pokhala ndi chikhulupiriro, Sara yemwe adalandira mphamvu zakutenga pathupi, ngakhale zaka zake zakubala mwana zinali zitapita kale. Zimenezi zidatheka chifukwa adaavomera kuti amene adazilonjezayo ngwokhulupirika. Nchifukwa chake mwa munthu mmodzi, wotinso anali ngati wakufa, mudatuluka mibadwo yochuluka ngati nyenyezi, ndi yosaŵerengeka ngati mchenga wa pa gombe la nyanja. Onseŵa adasunga chikhulupiriro chao mpaka kufa. Sadalandire zimene Mulungu adaaŵalonjeza, koma adangoziwonera chapatali ndi kuzikondwerera. Adaavomera kuti pansi pano analidi alendo osakhazikika. Paja anthu olankhula motere, amaonekeratu kuti akufunafuna malo ao enieni okhazikikamo. Akadakhala kuti ankaganizirako za kudziko kumene adaachokera, bwenzi atapeza danga lakuti abwerere kwakaleko. Koma monga zilirimu tikuwona kuti ankafuna dziko lina, lokoma kopambana, ndiye kuti dziko la Kumwamba. Nchifukwa chake Mulungu sachita manyazi kutchedwa Mulungu wao, popeza kuti Iye adaŵakonzera mzinda. Pokhala ndi chikhulupiriro, Abrahamu, pamene Mulungu adamuyesa, adapereka Isaki ngati nsembe. Ngakhale anali munthu woti Mulungu adaampatsa lonjezo, adakhala wokonzeka kupereka ngati nsembe mwana wake mmodzi yekhayo. Za mwana ameneyu Mulungu anali atanena kuti, “Mwa Isaki udzakhala ndi zidzukulu.” Abrahamu ankakhulupirira kuti Mulungu nkuukitsa munthu kwa akufa. Tsono tingathe kunena mofanizira kuti adamlandiranso Isakiyo ngati wouka kwa akufa. Pokhala ndi chikhulupiriro, Isaki adapemphera ana ake, Yakobe ndi Esau, madalitso am'tsogolo. Pokhala ndi chikhulupiriro, Yakobe pakufa, adadalitsa ana a Yosefe mmodzimmodzi. Pochita zimenezi anali atayedzamira pa ndodo yake, akupembedza Mulungu. Pokhala ndi chikhulupiriro, Yosefe ali pafupi kutsirizika, adanenapo za kutuluka kwa Aisraele mu Ejipito, naŵauziratu za m'mene adaayenera kudzachitira ndi mafupa ake. Pokhala ndi chikhulupiriro, atabadwa Mose, makolo ake adamubisa miyezi itatu, poona kuti mwana waoyo anali wokongola. Sadaope konse lamulo lamphamvu la mfumu. Pokhala ndi chikhulupiriro, Mose atakula adakana kutchedwa mdzukulu wa Farao, mfumu ya ku Ejipito. Iye adasankha kuzunzikira nawo limodzi ana a Mulungu, koposa kukondwerera zosangalatsa za uchimo kanthaŵi pang'ono. Adaaona kuti kuzunzika chifukwa cha Wodzozedwa wa Mulungu kunali chuma chachikulu koposa chuma chonse cha ku Ejipito, pakuti maso ake anali ndithu pa mphotho yakutsogolo. Pokhala ndi chikhulupiriro, Mose adachoka ku Ejipito, osaopa ukali wa mfumu, popeza kuti ankapirira ngati munthu woona Mulungu wosaonekayu. Pokhala ndi chikhulupiriro, adachita nawo chikondwerero cha Paska, nalamula kuti anthu awaze magazi pa zitseko kuti mngelo woononga ana achisamba uja asakhudze ana achisamba a Aisraele. Pokhala ndi chikhulupiriro, Aisraele adaoloka Nyanja Yofiira ngati pamtunda pouma. Koma Aejipito, kuti nawonso ayesere kuwoloka, adamizidwa. Pokhala ndi chikhulupiriro, malinga a mzinda wa Yeriko adagwa, Aisraele ataŵazungulira masiku asanu ndi aŵiri. Pokhala ndi chikhulupiriro, Rahabu, mkazi wadama uja, sadafe nawo limodzi anthu osamvera aja, pakuti adaaŵalandira bwino azondi aja kunyumba kwake. Kodi ndinenenso chiyani tsopano? Nthaŵi yachepa yoti ndinene za anthu enanso ambiri monga Gideoni, Balaki, Samisoni, Yefita, Davide, Samuele ndiponso aneneri. Pokhala ndi chikhulupiriro anthu ameneŵa adagonjetsa maufumu, adakhazikitsa chilungamo, ndipo adalandira zimene Mulungu adaaŵalonjeza. Ena adapuya mikango pakamwa, ena adazimitsa moto waukali, ndipo ena adapulumuka, osaphedwa ndi lupanga. Anali ofooka, koma adalandira mphamvu. Adasanduka ngwazi pa nkhondo, nathamangitsa magulu a ankhondo a adani ao. Akazi ena adalandiranso anthu ao amene adafa, ataŵaukitsa. Ena adazunzidwa koopsa mpaka kufa, osalola kuti aŵamasule, chifukwa chofuna kudzaukanso ndi moyo wabwino kopambana. Ena, anthu adaŵaseka ndi kuŵakwapula. Adamangidwa ndi maunyolo naponyedwa m'ndende. Ena adaŵapha pakuŵaponya miyala; ena adaŵacheka pakati; ndipo ena adaŵapha ndi lupanga. Ankayenda uku ndi uku atavala zikopa zankhosa kapena zambuzi, umphaŵi wokhawokha, anthu nkumaŵazunza ndi kuŵavutitsa. Anthu ameneŵa, pansi pano sipadaŵayenere! Ankangoyenda m'zipululu ndi m'mapiri namabisala m'mapanga ndi m'maenje apansi. Anthu onseŵa, ngakhale adaaŵachitira umboni wokoma chifukwa cha chikhulupiriro chao, sadalandire zimene Mulungu adaalonjeza. Ndiye kuti Mulungu anali ataganiziratu zotikonzera zabwino zopambana, kotero kuti sadafune kuti anthu onse aja asafikire ku ungwiro popanda ife. Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu. Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu. Muziganiza za Iye amene adapirira udani waukulu chotere wochokera kwa anthu ochimwa, kuti musafookere ndi kutaya mtima. Polimbana ndi uchimo, simudafike mpaka pokhetsa magazi. Mwaiŵala kodi mau olimbitsa mtima aja, amene Mulungu amakulankhulani ngati ana ake? Mauwo ndi aŵa: “Mwana wanga, usanyozere malango a Ambuye, kapena kutaya mtima pamene Iwo akudzudzula. Paja Ambuye amamlanga aliyense amene amamkonda, amakwapula mwana aliyense amene Iwo amamlandira.” Muzipirira masautso kuti muphunzirepo makhalidwe oyenera. Mulungu amakutengani ngati ana ake m'zochita zake zonse. Kodi nkale lonse analipo mwana amene bambo wake sadamlange? Ngati Mulungu sakulangani inuyo, monga amachitira ndi ana ake onse, ndiye kuti sindinu ana enieni, koma am'chigololo. Tinali nawo azibambo athu apansipano amene ankatilanga, ndipo tinkaŵalemekeza. Kwenikweni tsono tikadayenera kugonjera Mulungu, Atate a mizimu, kuti tikhale ndi moyo. Azibambo athu apansipanowo ankatilanga pa kanthaŵi kochepa kokha, akazindikira kuti nkofunika. Koma Mulungu amatilanga kuti tipindulepo, ndipo tilandireko kuyera mtima kwake. Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama. Limbitsani tsono manja anu ofooka ndiponso maondo anu agooka. Muziyenda m'njira zoongoka, kuti miyendo yopunduka isagweduke, koma ichiritsidwe. Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako. Chenjerani kuti wina aliyense asabwerere m'mbuyo nkutaya madalitso a Mulungu. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale ngati muzu woŵaŵa, umene umaphuka nkuvuta ena ambiri ndi ululu wake. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale wadama, kapena wonyoza zauzimu, monga Esau, amene adaagulitsa ukulu wake ndi chakudya cha kamodzi kokha. Paja mukudziŵa kuti, pambuyo pake adaafuna kulandira madalitso a atate ake, koma zidakanika, chifukwa sadathenso kusintha maganizo, ngakhale adaalakalaka kutero molira mizozi. Inu simudachite monga Aisraele aja, amene adaafika ku chinthu chimene adaatha kuchikhudza, ndiye kuti ku Phiri la Sinai, lija linali loyaka moto, lamdima wa bii, la mphepo yamkuntho; limene panali kulira kwa lipenga, ndiponso kumveka kwa mau. Anthu atamva mauwo, adaapempha kuti asaŵamvenso konse, pakuti lidaaŵaopsa lamulo lija lakuti, “Ndi nyama yomwe ikangokhudza phirilo, iphedwe ndi miyala.” Maonekedwe a zonsezo anali oopsa kwambiri, kotero kuti Mose yemwe adaati, “Ndikunjenjemera ndi mantha.” Koma inu mwafika ku Phiri la Ziyoni, ndiponso ku mzinda wa Mulungu wamoyo, ndiye kuti Yerusalemu wa Kumwamba, m'mene muli angelo osaŵerengeka. Mwafika kuchikondwerero kumene kwasonkhana ana oyamba a Mulungu, amene maina ao adalembedwa Kumwamba. Mwafika kwa Mulungu, mweruzi wa anthu onse, ndiponso kwa mizimu ya anthu olungama, amene Mulungu waŵasandutsa angwiro kwenikweni. Mwafika kwa Yesu, Nkhoswe yokonza za chipangano chatsopano, ndiponso mwafika ku magazi okhetsedwa, amene akutilonjeza zinthu zabwino koposa m'mene magazi a Abele ankachitira. Chenjerani tsono kuti musakane kumvera amene akulankhula nanu. Anthu amene adakana kumvera iye uja amene adaaŵachenjeza pansi pano, sadapulumuke ku chilango ai. Nanji tsono ifeyo, tidzapulumuka bwanji ngati timufulatira wotilankhula kuchokera Kumwambaku? Nthaŵi imeneyo mau a Mulungu adaagwedeza dziko, koma tsopano lino walonjeza ndi mau akuti, “Kamodzi kenanso ndidzagwedeza, osati dziko lokha ai, koma ndi thambo lomwe.” Mau akuti “Kamodzi kenanso” akuwonetsa poyera kuti zolengedwa zonse zogwedezeka zidzachotsedwa, kuti zinthu zosagwedezeka zidzakhalitse. Popeza kuti talandira ufumu wosagwedezeka, tizithokoza Mulungu, ndipo pakutero timpembedze moyenera, mwaulemu ndi mwamantha. Paja Mulungu wathu ndi moto wopsereza. Pitirizani kukondana monga abale. Musanyozere kumalandira bwino alendo m'nyumba mwanu. Pali ena amene kale adaalandira bwino alendo, ndipo mosazindikira adaalandira angelo. Muzikumbukira am'ndende, ngati kuti mukuzunzikira nawo limodzi m'ndendemo. Muzikumbukira ovutitsidwa, pakuti inunso muli ndi thupi. Ukwati muziwulemekeza nonse, ndipo amuna ndi akazi ao azikhala okhulupirika, pakuti anthu adama ndi achigololo Mulungu adzaŵalanga. Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.” Tiyeni tsono tilimbe mtima ndi kunena kuti, “Ambuye ndiwo Mthandizi wanga, sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani?” Muzikumbukira atsogoleri anu amene ankakulalikirani mau a Mulungu. Muzilingalira za moyo wao ndi m'mene adafera, ndipo muzitsanzira chikhulupiriro chao. Yesu Khristu ndi yemweyo dzulo, lero ndi mpaka muyaya. Musalole zophunzitsa zosiyanasiyana ndiponso zachilendo kuti zikusokeretseni. Choyenera kutilimbitsa mtima ndi kukoma mtima kwa Mulungu, osati malamulo onena za chakudya ai. Malamulo ameneŵa sadaŵapindulitsepo anthu amene ankaŵatsata. Ife tili ndi guwa, ndipo ansembe otumikira m'chihema chachipembedzo cha Ayuda saloledwa kudyako zoperekedwa pamenepo. Mkulu wa ansembe wachiyuda amaloŵa ndi magazi a nyama ku Malo Opatulika kuti magaziwo akhale nsembe yopepesera machimo. Koma nyama yeniyeniyo amaiwotchera kunja kwa misasa. Chifukwa cha chimenechi, Yesu nayenso adafera kunja kwa mzinda, kuti pakutero ayeretse anthu ndi magazi ake. Tiyeni tsono tipite kwa Iye kunja kwa misasa kuti tikanyozekere naye limodzi. Paja ife tilibe mzinda wokhazikika pansi pano, tikufunafuna wina umene ulikudza. Nchifukwa chake, kudzera mwa Yesu tiyeni tipereke kosalekeza mayamiko athu kwa Mulungu ngati nsembe. Ndiye kunena kuti tipereke ngati nsembe mau athu ovomereza dzina lake poyera. Musanyozere kumachita zachifundo ndi kumathandizana, chifukwa nsembe zotere zimakondweretsa Mulungu. Muzimvera atsogoleri anu ndi kuŵagonjera. Iwo sapumulira konse poyang'anira moyo wanu, pakuti adzayenera kufotokoza za ntchito yao pamaso pa Mulungu. Mukaŵamvera, adzagwira ntchito yaoyo mokondwa osati monyinyirika, kupanda kutero ndiye kuti kwa inuyo phindu palibe. Muzitipempherera ifeyo, pakuti sitipeneka konse kuti tili ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa, ndipo tatsimikiza kuchita zonse mwachilungamo. Ndikukupemphani makamaka kuti mupemphere kuti Mulungu andibwezere kwa inu msanga. Mulungu wopatsa mtendere, adaukitsa kwa akufa Ambuye athu Yesu, amene ndiye Mbusa wamkulu wa nkhosa, chifukwa cha imfa yake yotsimikizira Chipangano chamuyaya. Mulunguyo akupatseni zabwino zonse zimene mukusoŵa kuti muzichita zimene Iye afuna. Ndipo mwa Yesu Khristu achite mwa ife zomkondweretsa, Khristuyo akhale ndi ulemerero mpaka muyaya. Amen. Ndikukupemphani, inu abale anga, kuti muŵalandire bwino mau okulimbitsani mtimaŵa, pakuti ndangokulemberani mwachidule. Ndikufuna kuti mudziŵe kuti Timoteo, mbale wathu, amtulutsa m'ndende. Akafika msanga, ndidzabwera naye kwanuko podzakuwonani. Mutiperekereko moni kwa atsogoleri anu onse, ndi kwa anthu onse a Mulungu. Abale a ku Italiya akuti moni. Mulungu akukomereni mtima nonse. Ndine, Yakobe, mtumiki wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu. Ndikupereka moni kwa inu anthu a Mulungu, a mafuko khumi ndi aŵiri, obalalikana ku maiko osiyanasiyana. Abale anga, muzikondwa ndithu mukamayesedwa ndi mavuto amitundumitundu. Paja mukudziŵa kuti mukamayesedwa m'chikhulupiriro chanu, mumasanduka olimbika. Koma kulimbika kumeneku kuzigwira ntchito yake kotheratu, kuti mukhale angwiro, opanda chilema ndi osapereŵera pa kanthu kalikonse. Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera. Koma wopemphayo apemphe mokhulupirira, ndi mosakayika konse. Paja munthu wokayikakayika ali ngati mafunde apanyanja, amene amavunduka ndi kuŵinduka ndi mphepo. Munthu wotere asamaganiza kuti nkudzalandira kanthu kwa Ambuye ai; pakuti iyeyo ndi wa mitima iŵiri, ndi wosakhazikika pa zochita zake zonse. Mbale woluluka anyadire pamene Mulungu amkweza. Ndipo mbale wolemera nayenso anyadire pamene Mulungu amtsitsa, pakuti adzatha ngati duŵa la udzu. Dzuŵa limatuluka nkutentha kwake, ndipo limaumitsa udzu. Duŵa la udzuwo limathothoka, kukongola kwake nkutha. Chomwechonso moyo wa wolemerayo udzazimirira ali pakati pa zochita zake. Ngwodala munthu amene amalimbika pamene ayesedwa, pakuti atapambana, adzalandira moyo. Moyowo ndi mphotho imene Ambuye adalonjeza anthu oŵakonda. Pamene munthu akuyesedwa ndi zinyengo, asanene kuti, “Mulungu akundiika m'chinyengo.” Paja Mulungu sangathe kuyesedwa ndi zinyengo, ndipo Iyeiyeyo saika munthu aliyense m'chinyengo. Koma munthu aliyense amayesedwa ndi zinyengo pamene chilakolako cha mwiniwakeyo chimkopa ndi kumkola. Pamenepo chilakolakocho chimachita ngati chatenga pathupi nkubala uchimo. Tsono uchimowo utakula msinkhu, umabala imfa. Musamanyengedwa, abale anga okondedwa. Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera Kumwamba, kwa Atate a zounikira zonse zakuthambo. Iwo sasinthika konse, ndipo kuŵala kwao sikutsitirika mpang'ono pomwe. Mwa kufuna kwake mwiniwakeyo, adatipatsa moyo kudzera mwa mau ake oona, kuti pakati pa zolengedwa zake zonse, ife tikhale ngati zipatso zoyamba zimene Iye wadzipatulira. Abale anga okondedwa, gwiritsani mau aŵa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma kulankhula asamafulumira, ndipo kukwiya asamafulumiranso. Paja munthu wokwiya safikapo pa chilungamo chimene amafuna Mulungu. Nchifukwa chake siyani chizoloŵezi chilichonse chonyansa, ndiponso kuipamtima kulikonse. Muŵalandire mofatsa mau amene Mulungu adabzala m'mitima mwanu, pakuti ndiwo angathe kukupulumutsani. Musamadzinyenga pakungomva chabe mau a Mulungu, koma muzichita zimene mauwo anena. Paja munthu amene amangomva chabe mau, osachita zimene wamvazo, ali ngati munthu woyang'anira nkhope yake yachibadwa m'galasi. Tsono amati akadzipenya, amachokapo, posachedwa nkuiŵalako m'mene akuwonekera. Malamulo a Mulungu ndi angwiro ndiponso opatsa anthu ufulu. Munthu amene amalandira Malamulowo nkumaŵatsata mosamala, amene samangomva mau nkuŵaiŵala, koma amaŵagwiritsa ntchito, ameneyo Mulungu adzamdalitsa pa zochita zake zonse. Ngati wina akudziyesa woika mtima pa zopembedza Mulungu, koma nkukhala wosasunga pakamwa, chipembedzo chakecho nchopanda pake, ndipo amangodzinyenga. Chipembedzo choona ndi changwiro pamaso pa Mulungu amene ali Atate, ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto ao, ndiponso kudzisunga bwino, kuwopa kudetsedwa ndi zoipa za m'dziko lapansi. Abale anga, popeza kuti mumakhulupirira Ambuye athu Yesu Khristu, Ambuye aulemerero, musamakondera. Mwachitsanzo: munthu wina aloŵa mumsonkhano mwanu atavala mphete zagolide m'manja, alinso ndi zovala zokongola. Winanso nkuloŵa, koma ali mmphaŵi, nsanza zili wirawira. Tsono inu pofuna kusamala kwambiri wovala zokongolayo, mumuuza kuti, “Khalani apa pabwinopa”, mmphaŵi uja nkumuuza kuti, “Iwe, kaimirire apo, kapena dzakhale pansi kumapazi kwangaku.” Limenelotu ndi tsankho pakati pa inu nokhanokha, ndipo inuyo mwasanduka oweruza a maganizo oipa. Mverani, abale anga okondedwa, kodi suja Mulungu adasankha ooneka amphaŵi m'maso mwa anthu, kuti akhale olemera pa chikhulupiriro, ndi kuti alandire madalitso amene Iye adalonjeza anthu omukonda? Koma inuyo mwakhala mukumnyoza mmphaŵiyo. Kodi si anthu olemera amene amakupsinjani? Si anthu olemera kodi amene amakukokerani ku mabwalo amilandu? Kodi si omwewo amene amalichita chipongwe dzina lolemekezekali la Khristu, limene inu mumatchulidwa? Tsono mumachita bwino ngati mumatsatadi lamulo lachifumu lija limene limapezeka m'Malembo, lonena kuti, “Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.” Koma mukamaonetsa kukondera, mukuchimwa, ndipo Malamulo a Mulungu akukutsutsani kuti ndinu opalamula. Pajatu munthu wotsata Malamulo onse, akangophonyapo ngakhale pa mfundo imodzi yokha, ndiye kuti wachimwira Malamulo onsewo. Pakuti Mulungu amene adanena kuti, “Usachite chigololo”, adanenanso kuti, “Usaphe”. Ngati inu chigololo simuchita, koma kupha mumapha, ndiye kutitu mwachimwira Malamulo onse. Tsono muzilankhula ndi kuchita zinthu monga anthu oti Mulungu adzaŵaweruza potsata lamulo loŵapatsa ufulu. Paja munthu woweruza mopanda chifundo, nayenso Mulungu adzamuweruza mopanda chifundo. Koma wochita chifundo alibe chifukwa choopera chiweruzo cha Mulungu. Abale anga, pali phindu lanji, ngati munthu anena kuti, “Ndili ndi chikhulupiriro,” koma popanda chimene akuchitapo? Kodi chikhulupiriro chotere chingampulumutse? Mwachitsanzo: mbale wina kapena mlongo ali ndi usiŵa, ndipo masiku onse alibe chakudya chokwanira. Tsono wina mwa inu angoŵauza kuti. “Pitani ndi mtendere, mukafundidwe ndipo mukakhute”, koma osaŵapatsa zimene akusoŵazo, pamenepo phindu lake nchiyani? Choncho, chikhulupiriro pachokha, chopanda ntchito zake, nchakufa basi. Koma kapena wina anganene kuti, “Inuyo muli ndi chikhulupiriro, ineyo ndili ndi ntchito zabwino.” Pamenepo ine nkumuyankha kuti, “Uyesetse kundiwonetsa chikhulupiriro chako chopanda ntchito zakecho, ine ndi ntchito zanga ndikuwonetsa chikhulupiriro changa.” Inu mumakhulupirira kuti Mulungu ndi mmodzi yekha. Ai chabwino, mumakhoza, komatu ndi mizimu yoipa yomwe imakhulupirira zimenezi, imachitanso kunjenjemera. Wopusawe, kodi ukufuna umboni wotsimikiza kuti chikhulupiriro chopanda ntchito zake nchachabe? Nanga Abrahamu, kholo lathu, suja adakhala wolungama pamaso pa Mulungu chifukwa cha ntchito yomwe adachita, muja adaapereka mwana wake Isaki pa guwa lansembe? Waona tsono kuti chikhulupiriro chake ndi zochita zake zidachitikira pamodzi. Zochita zake zidasandutsa chikhulupiriro chake kuti chifike pake penipeni. Motero zidachitikadi zimene Malembo adaanena, kuti, “Abrahamu adakhulupirira Mulungu, nchifukwa chake Mulungu adamuwona kuti ngwolungama;” mwakuti ankatchedwa bwenzi la Mulungu. Mukuwonatu kuti zochita zake za munthu ndizo zimamsandutsa wolungama pamaso pa Mulungu, osati chikhulupiriro chokha. Kodi suja zidaateronso ndi Rahabu, mkazi wadama uja? Iye adaalandira azondi aja, nkuŵabweza kwao poŵadzeretsa njira ina, ndipo adapezeka kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu chifukwa cha zimene adaachitazo. Paja monga momwe thupi lopanda mzimu limakhala lakufa, moteronso chikhulupiriro chopanda ntchito zake nchakufa. Abale anga, musachuluke ofuna kukhala aphunzitsi, chifukwa monga mudziŵa, aphunzitsife tidzaweruzidwa mouma koposa anthu ena onse. Paja tonsefe timalakwa pa zinthu zambiri. Ngati alipo amene salakwa pakulankhula, ndiye kuti ndi wangwirodi ameneyo, mwakuti angathe kulamuliranso thupi lake lonse. Timaika kachitsulo m'kamwa mwa kavalo kuti atimvere, ndipo tingathe kumaongolera thupi lake lonse. Onaninso zombo. Ngakhale nzazikulu kwambiri, ndipo zimakankhidwa ndi mphepo yamphamvu, komabe tsigiro laling'onong'ono ndi limene limaziwongolera kulikonse kumene woyendetsa akufuna. Chimodzimodzinso lilime: ndi kachiwalo kakang'ono, komabe limadzitama kuti nkuchita zazikulu. Tangoganizani kukula kwake kwa nkhalango imene ingayatsidwe ndi kalilaŵi kakang'ono ka moto. Tsonotu lilime limatentha ngati moto. Chifukwa chokhala pakati pa ziwalo zathu limawanditsa zoipa m'thupi monse. Limaipitsa khalidwe lonse la munthu. Limayatsa moto moyo wathu wonse kuyambira pobadwa mpaka imfa; ndipo moto wake ngwochokera ku Gehena. Munthu angathe kuŵeta mtundu uliwonse wa nyama, wa mbalame, wa zokwaŵa, ndi wazam'nyanja, ndipo adaziŵetapodi. Koma lilime palibe munthu amene angathe kuliŵeta. Ndi loipa, silidziŵa kupumula, ndipo ndi lodzaza ndi ululu wakupha. Ndi lilime lomwelo timayamika Ambuye, amenenso ndi Atate, komanso ndi lilime lomwelo timatemberera anthu anzathu amene Mulungu adaŵalenga ofanafana naye. Pakamwa pomwe pamatuluka mayamiko pomweponso pamatuluka matemberero. Abale anga, zoterezi siziyenera kumachitika. Kodi kasupe amatulutsa madzi omweka ndi oŵaŵa pa dzenje limodzimodzi? Abale anga, kodi mkuyu ungathe kubala zipatso za olivi, kapena mpesa kubala nkhuyu? Momwemonso kasupe wa madzi amchere sangathe kupereka madzi omweka. Ndani mwa inu ali wanzeru ndi womvetsa zinthu? Aonetse ndi makhalidwe ake abwino kuti nzeru zimaongoleradi zochita zake zofatsa. Koma ngati muli ndi mtima wakaduka ndi wodzikonda, musamanyada ndi kutsutsana ndi choona pakunena mabodza. Nzeru zotere si zochokera Kumwamba, koma ndi nzapansipano, ndi za anthu chabe, ndiponso nzochokera ku mizimu yoipa. Pajatu pamene pali kaduka ndi kudzikonda, pomweponso pali chisokonezo ndi ntchito yoipa ya mtundu uliwonse. Koma nzeru zochokera Kumwamba, poyamba nzangwiro, kuwonjeza apo nzamtendere, zofatsa ndi zomvera bwino. Ndi za chifundo chambiri, ndipo zipatso zake zabwino nzochuluka. Nzeruzo sizikondera kapena kuchita chiphamaso. Ndipo chilungamo ndiye chipatso cha mbeu zimene anthu odzetsa mtendere amafesa mu mtendere. Kodi nkhondo zimachokera kuti? Kukangana pakati panu kumachokera kuti? Kodi suja zimachokera ku zilakolako zanu zathupi, zimene zimachita nkhondo mwa inu? Mumalakalaka zinthu, koma zimakusoŵani, nchifukwa chake mumapha munthu. Mumasirira zinthu, koma simungathe kuzipeza, nchifukwa chake mumamenyana, nkumachita nkhondo. Mulibe zinthuzo chifukwa simupempha kwa Mulungu. Ndipo ngakhale mupemphe, simulandira, chifukwa mumapempha molakwa. Zimene mumapempha, mumafuna kungozimwazira pa zokukondweretsani basi. Inu anthu osakhulupirikanu, kodi simudziŵa kuti kuchita chibwenzi ndi zapansipano nkudana ndi Mulungu? Choncho munthu wofuna kukhala bwenzi la zapansipano, ameneyo amadzisandutsa mdani wa Mulungu. Kodi kapena mukuyesa kuti Malembo amanena pachabe kuti, “Mulungu amafunitsitsa mwansanje mzimu umene Iye adaika kuti uzikhala mwa ife?” Koma amatikomera mtima koposa. Nchifukwa chake Malembo akuti, “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma odzichepetsa amaŵakomera mtima.” Tsono muzigonjera Mulungu. Satana muzilimbana naye, ndipo adzakuthaŵani. Yandikirani kwa Mulungu, ndipo Iye adzayandikira kwa inu. Muzisamba m'manja, inu anthu ochimwa. Chotsani maganizo onyenga m'mitima mwanu, inu anthu okayikakayika. Zindikirani umphaŵi wanu, imvani chisoni, lirani misozi. Kuseka kwanu kusanduke kulira, ndipo chimwemwe chanu chisanduke chisoni. Mudzichepetse pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani. Abale, musamasinjirirana. Wosinjirira mbale wake kapena kumuweruza, akusinjirira ndi kuweruza Malamulo a Mulungu. Koma ukaweruza Malamulo a Mulungu, ndiye kuti sukuchita zimene Malamulowo akunena, ukudziyesa woweruza. Mulungu yekha ndiye wopanga Malamulo ndiponso woweruza. Ndiyenso wotha kupulumutsa ndi kuwononga. Nanga iwe ndiwe yani kuti uziweruza mnzako? Onani tsono, inu amene mukuti, “Lero kapena maŵa tipita ku mzinda wakutiwakuti, ndipo tikachitako malonda chaka chimodzi kuti tikaphe ndalama,” m'menemo inuyo zamaŵa simukuzidziŵa. Kodi moyo wanu ngwotani? Pajatu inu muli ngati utsi chabe, umene umangooneka pa kanthaŵi, posachedwa nkuzimirira. Kwenikweni muyenera kumanena kuti, “Ambuye akalola, tikakhala ndi moyo, tidzachita chakutichakuti.” Koma monga zilirimu, mumanyada ndi kudzitama. Kunyada konse kotere nkoipa. Munthu akadziŵa zabwino zimene ayenera kuchita, napanda kuzichita, ndiye kuti wachimwa. Mverani tsono, inu anthu achumanu. Lirani ndi kufuula chifukwa cha zovuta zimene zikudzakugwerani. Chuma chanu chaola, ndipo njenjete zadya zovala zanu. Golide wanu ndi siliva zachita dzimbiri, ndipo dzimbirilo lidzakhala mboni yokutsutsani. Lidzaononga thupi lanu ngati moto. Mwadziwunjikira chuma pa masiku ano amene ali otsiriza. Antchito okolola m'minda mwanu simudaŵalipire. Ndalama zamalipirozo zikulira mokutsutsani. Ndipo kufuula kwa okololawo kwamveka m'makutu a Chauta Mphambe. Mwakhala mukuchita maphwando, ndipo mwalidyera dziko lino lapansi. Mwadzinenepetsa pa tsiku lopha anthu. Mwamuweruza kuti ngwolakwa ndipo mwamupha munthu wolungama, iye osalimbalimba. Tsono abale, khazikani mtima pansi mpaka Ambuye adzabwere. Onani m'mene amachitira mlimi. Amadikira kuti zipatso zokoma ziwoneke m'munda mwake. Amangoyembekeza mokhazika mtima kuti zilandire mvula yachizimalupsa ndi yachikokololansanu. Inunso khazikani mtima. Limbani mtima, pakuti Ambuye ali pafupi kubwera. Abale musamanenerana zoipa pakati panu, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni. Onani, woweruza waima pa khomo. Abale, kumbukirani chitsanzo cha aneneri amene adalankhula m'dzina la Ambuye. Iwo adamva zoŵaŵa, komabe adapirira. Anthu amene timaŵatchula odala, ndi amene anali olimbika. Mudamva za kulimbika kwa Yobe, ndipo mudaona m'mene Ambuye adamchitira potsiriza, pakuti Ambuye ngachifundo ndi okoma mtima. Koma koposa zonse abale anga, musamalumbira. Musalumbire potchula Kumwamba, kapena dziko lapansi, kapena china chilichonse. Pofuna kutsimikiza kanthu, muzingoti, “Inde”. Pofuna kukana kanthu, muzingoti, “Ai”. Muzitero, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni kuti ndinu opalamula. Kodi wina mwa inu ali m'mavuto? Apemphere. Kodi wina wakondwa? Aimbe nyimbo zotamanda Mulungu. Kodi wina mwa inu akudwala? Aitanitse akulu a mpingo. Iwowo adzampempherere ndi kumdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye. Akampempherera ndi chikhulupiriro, wodwalayo adzapulumuka, Ambuye adzamuutsa, ndipo ngati anali atachimwa, Ambuye adzamkhululukira machimowo. Muziwululirana machimo anu, ndipo muzipemphererana kuti muchire. Pemphero la munthu wolungama limakhala lamphamvu, ndipo silipita pachabe. Eliya anali munthu monga ife tomwe. Iye uja adaapemphera kolimba kuti mvula isagwe, ndipo mvula siidagwedi pa zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi. Atapempheranso, mvula idagwa, nthaka nkuyambanso kumeretsa mbeu zake. Abale anga, wina mwa inu akasokera pa kusiya choona, mnzake nkumubweza, dziŵani kuti amene adzabweza munthu wochimwa ku njira yake yosokera, adzapulumutsa moyo wa munthuyo ku imfa, ndipo chifukwa cha iye machimo ochuluka adzakhululukidwa. Ndine, Petro, mtumwi wa Yesu Khristu. Ndikulemba kalatayi kwa inu osankhidwa a Mulungu, amene muli obalalikira ku chilendo, ku maiko a ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asiya ndi Bitiniya. Mulungu Atate adakusankhani, monga Iye adaziganiziratu kuyambira pa chiyambi, kuti Mzimu Woyera akuyeretseni ndipo kuti mumvere Yesu Khristu, ndi kutsukidwa ndi magazi ake. Mulungu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere wonka nuchulukirachulukira. Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Iye mwa chifundo chake chachikulu adatibadwitsanso pakuukitsa Yesu Khristu kwa akufa. Motero timakhulupirira molimba mtima kuti tidzalandira ngati choloŵa zokoma zosaonongeka, zosaipitsidwa, ndi zosafota, zimene Mulungu akukusungirani Kumwamba. Ndi mphamvu zake Mulungu akukusungani inunso omkhulupirira, kuti mudzalandire chipulumutso chimene Iye ali wokonzeka kuchiwonetsa pa nthaŵi yotsiriza. Zimenezi zikukondweretseni, ngakhale tsopano mumve zoŵaŵa poyesedwa mosiyanasiyana pa kanthaŵi. Monga golide, ngakhale ndi wotha kuwonongeka, amayesedwa ndi moto, momwemonso chikhulupiriro chanu, chimene nchoposa golide kutali, chimayesedwa, kuti chitsimikizike kuti nchenicheni. Apo ndiye mudzalandire chiyamiko, ulemerero ndi ulemu pamene Yesu Khristu adzaoneka. Iyeyu simudamuwone, komabe mumamkonda. Ngakhale simukumuwona tsopano, mumamkhulupirira ndipo mumakondwera ndi chimwemwe chachikulu ndi chosaneneka. Pakutero mukupata mphotho ya chikhulupiriro, ndiye kuti chipulumutso chanu. Aneneri amene adaneneratu za mphotho yaulere imene mudzalandireyo, ankafunafuna mofufuzafufuza za chipulumutsochi. Mzimu wa Khristu wokhala mwa iwo ankaneneratu za zoŵaŵa zimene Khristu adzamve, ndiponso za ulemerero umene adzakhale nawo pambuyo pake. Aneneriwo ankafunafuna kudziŵa kuti kodi zimenezi zidzachitika liti, ndiponso mwa njira yanji. Mulungu adaŵaululira kuti ntchito yaoyi sankaigwira chifukwa cha eniakewo, koma chifukwa cha inu, pamene iwo ankanena zoonazi zimene mwamva tsopano. Olalika Uthenga Wabwino adakuuzani zoonazi mwa mphamvu ya Mzimu Woyera wotumidwa kuchokera Kumwamba. Angelo omwe amalakalaka kuwona nao zinthuzo. Nchifukwa chake mtima wanu ukhale wokonzeka. Khalani tchelu. Khazikitsani chiyembekezo chanu kotheratu pa kukoma mtima kwa Mulungu pamene Yesu Khristu adzaoneke. Muzikhala ngati ana omvera, osatsatanso zimene munkalakalaka pamene munali osadziŵa. Koma monga Iye amene adakuitanani ali woyera mtima, inunso khalani oyera mtima m'makhalidwe anu onse. Paja mau a Mulungu akuti, “Muzikhala oyera mtima popeza kuti Ineyo ndine woyera mtima.” Mulungu alibe tsankho. Amaweruza aliyense molingana ndi zochita zake. Ngati mumutcha Atate pamene mukupemphera, mchitireni ulemu nthaŵi yonse muli alendo pansi pano. Mukudziŵa bwino chimene adakuwombola nachoni ku khalidwe lanu lachabe limene mudalandira kwa makolo anu. Sadakuwomboleni ndi ndalama zotha kuwonongeka zija, siliva kapena golide ai, adakuwombolani ndi magazi amtengowapatali a Khristu amene adakhala ngati mwanawankhosa wopanda banga kapena chilema. Iyeyo Mulungu adaamsankhiratu dziko lapansi lisanalengedwe, koma wamuwonetsa nthaŵi yotsiriza ino chifukwa cha inu. Kudzera mwa Iye mumakhulupirira Mulungu amene adamuukitsa kwa akufa, namupatsa ulemerero. Ndipo choncho chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu zili mwa Mulungu. Mwayeretsa mitima yanu pakumvera choona, kotero kuti muzikondana ndi akhristu anzanu mosanyenga. Nchifukwa chake muzikondana ndi mtima wonse, mosafookera. Pakuti mwa mwachita kubadwanso, moyo wake si wochokera m'mbeu yotha kuwonongeka, koma m'mbeu yosatha kuwonongeka. Mbeuyi ndi mau a Mulungu, mau amoyo ndi okhala mpakampaka. Paja mau a Mulungu amanena kuti, “Anthu onse ali ngati udzu, ulemerero wao uli ngati duŵa lakuthengo. Udzu umauma, ndipo duŵa limathothoka, koma mau a Ambuye ngokhala mpaka muyaya.” Mau ameneŵa ndi Uthenga Wabwino umene walalikidwa kwa inu. Nchifukwa chake tayani choipa chonse, kunyenga konse, chiphamaso, kaduka ndi masinjiriro onse. Monga makanda obadwa chatsopano amalirira mkaka, inunso muzilakalaka mkaka weniweni wodyetsa mtima wanu, kuti ukukuzeni ndi kukufikitsani ku chipulumutso, popeza kuti mwachilaŵadi chifundo cha Ambuye. Bwerani kwa Iye amene ali mwala wamoyo womwe anthu adaukana, koma Mulungu adausankha kuti ngwamtengowapatali. Inunso mukhale ngati miyala yamoyo yoti Mulungu amangire nyumba yake. M'menemo muzitumikira ngati ansembe opatulika, pakupereka nsembe zochokera ku mtima, zokomera Mulungu kudzera mwa Yesu Khristu. Paja m'Malembo mudalembedwa kuti. “Ndasankha mwala wamtengowapatali. Ndikuuika tsopano m'Ziyoni, ngati mwala wapangodya. Wokhulupirira Iye sadzachita manyazi.” Tsono kwa inu okhulupirira, Iye ndi wamtengowapatali. Koma kwa osakhulupirira, ndi monga momwe mau a Mulungu anenera kuti, “Mwala womwe amisiri omanga nyumba adaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya.” Mau a Mulungu akutinso, “Umenewu ndi mwala wokhumudwitsa anthu, ndi thanthwe loŵagwetsa.” Amakhumudwa popeza kuti amakana kumvera mau a Mulungu, ndipo anali oyeneradi kuti adzaone zotere. Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa. Kale simunali anthu a Mulungu, koma tsopano ndinu anthu ake. Kale simudaalandira chifundo, koma tsopano mwachilandira. Okondedwa anga, popeza kuti ndinu alendo pansi pano, ndikukupemphani kuti musagonjere zilakolako zathupi zimene zimachita nkhondo ndi mzimu wanu. Samalani mayendedwe anu pakati pa akunja, kuti ngakhale azikusinjirirani kuti ndinu anthu ochita zoipa, komabe aziwona ntchito zanu zabwino. Apo adzalemekeza Mulungu pa tsiku limene Iye adzaŵayendere. Chifukwa cha Ambuye, muzimvera akulu onse olandira ulamuliro. Ngati ndi mfumu yaikulu koposa ija, imvereni chifukwa ili ndi ulamuliro pa mafumu ena onse. Ngati ndi nduna, zimvereni chifukwa zidachita kutumidwa ndi mfumu kuti zizilanga ochita zoipa ndi kuyamikira ochita zabwino. Paja Mulungu amafuna kuti ndi zochita zanu zabwino muthetse kulankhula kosadziŵa kwa anthu opusa. Inde muzikhala ngati mfulu, koma ufulu wanuwo usakhale ngati chinthu chophimbira zoipa. Koma khalani ngati atumiki a Mulungu. Muzilemekeza anthu onse. Muzikonda akhristu anzanu. Khalani anthu oopa Mulungu. Mfumu yaikulu koposa ija muziipatsa ulemu. Inu antchito, muzimvera ndi ulemu wonse anthu okulembani ntchito, osati okhawo amene ali abwino ndi ofatsa ai, koma ndi ovuta omwe. Pajatu ndi chinthu chabwino ngati munthu, chifukwa chokumbukira Mulungu, apirira zoŵaŵa zosamuyenera. Kodi pali chiyani choti nkukuyamikirani ngati mupirira pamene akumenyani chifukwa choti mwachimwa? Koma mukapirira zoŵaŵa mutachita zabwino, apo mwachita chinthu chovomerezedwa ndi Mulungu. Mkhalidwe wotere ndi umene Mulungu adakuitanirani. Paja Khristu nayenso adamva zoŵaŵa chifukwa cha inu, nakusiyirani chitsanzo kuti muzilondola mapazi ake. Iye sadachitepo tchimo lililonse, ndipo sadanene bodza lililonse. Pamene anthu ankamuchita chipongwe, Iye sadabwezere chipongwe. Pamene ankazunzika, Iye sadaopseze, koma adapereka zonse kwa Mulungu amene amaweruza molungama. Khristu mwiniwake adasenza machimo athu m'thupi lake pa mtanda, kuti m'machimo tikhale ngati akufa, koma pakutsata chilungamo tikhale amoyo ndithu. Mudachiritsidwa ndi mabala ake. Munali ngati nkhosa zosokera, koma tsopano mwabwerera kwa Mbusa amene ndi wokuyang'anirani. Chimodzimodzinso inu azimai, muzimvera amuna anu, kuti ngati ena mwa iwo samvera mau a Mulungu, azikopeka ndi makhalidwe a akazi aonu. Sipadzafunikanso kunenerera mau, popeza kuti adzadziwonera okha makhalidwe anu aulemu ndi angwiro. Kudzikongoletsa kwanu kusangokhala kwa maonekedwe akunja pakuluka tsitsi, ndi kuvala zamakaka zagolide ndi zovala zamtengowapatali. Koma kudzikongoletsa kwanu kukhale kwa moyo wam'kati, kukongola kosatha kwa mtima wofatsa ndi wachete. Moyo wotere ngwamtengowapatali pamaso pa Mulungu. Umu ndi m'mene kale lija azimai oyera mtima okhulupirira Mulungu ankadzikongoletsera, ndipo ankamvera amuna ao. Sara yemwe ankamvera Abrahamu, ndi kumutcha “Mbuyanga.” Motero inu azimai, ndinu ana ake a Sarayo, ngati muchita bwino, osalola kuwopsedwa ndi kanthu kalikonse. Inunso amuna, muzikhala moŵamvetsa bwino akazi anu. Muziŵachitira ulemu popeza kuti iwowo ndi mtundu wofookerapo, ndiponso ngolandira nanu pamodzi mphatso ya Mulungu, imene ili moyo wosatha. Muzitero, kuti pasakhale kanthu koletsa mapemphero anu. Mau otsiriza ndi aŵa: nonse mukhale a mtima umodzi, ndi omverana chisoni. Muzikondana nawo abale. Mukhale a mtima wachifundo ndi odzichepetsa. Anthu okuchitani choipa, osaŵabwezera choipa, okuchitani chipongwe osaŵabwezera chipongwe. Koma inu muziŵadalitsa, pakuti inuyo Mulungu adakuitanirani mkhalidwe wotere, kuti mulandire madalitso ake. Paja mau a Mulungu akuti. “Yemwe afuna kukondwera ndi moyo, ndi kuwona masiku abwino, aletse lilime lake kulankhula zoipa, ndiponso milomo yake kunena mabodza. Alewe zoipa, azichita zabwino. Afunefune mtendere ndi kuyesetsa kuupeza. Paja Ambuye amaŵayang'anira bwino anthu olungama amatchera khutu ku mapemphero ao. Koma ochita zoipa saŵayang'ana bwino.” Ndani angakuchiteni choipa ngati muchita changu pa zabwino? Koma ngakhale mumve zoŵaŵa chifukwa cha chilungamo, mudzakhala odala ndithu. Musachite mantha ndi anthu, kapena kuvutika mu mtima, koma muzilemekeza Khristu m'mitima mwanu ngati Mbuye wanu. Khalani okonzeka nthaŵi iliyonse kuŵayankha mofatsa ndi mwaulemu anthu okufunsani za zimene mumayembekeza. Khalani ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa, kotero kuti anthu ena akamasinjirira mayendedwe anu abwino pamene mukutsata Khristu, achite manyazi ndi chipongwe chao. Nkwabwino kumva zoŵaŵa chifukwa chochita zabwino, ngati Mulungu wafuna choncho, koposa kumva zoŵaŵa chifukwa chochita zoipa. Paja nayenso Khristu adafera machimo a anthu kamodzi kokha; munthu wolungama kufa m'malo mwa anthu ochimwafe, kuti atifikitse kwa Mulungu. Pa za thupi adaphedwa, koma pa za mzimu adapatsidwa moyo. Ndipo ali ngati mzimu choncho, adapita kukalalika kwa mizimu imene inali m'ndende. Mizimuyi ndi ya anthu amene kale lija sadamvere pamene Mulungu adaadikira moleza mtima, pa nthaŵi imene Nowa ankapanga chombo. M'chombomo anthu oŵerengeka okha, asanu ndi atatu, adapulumuka ndi madzi. Madziwo akufanizira ubatizo umene masiku ano umakupulumutsani chifukwa cha kuuka kwa Yesu Khristu. Kubatizidwa kumeneku si kuchotsedwa litsiro la m'thupi, koma kudzipereka kwa Mulungu ndi mtima woona, kudzera mwa Yesu Khristu amene adapita Kumwamba, ndipo ali ku dzanja lamanja la Mulungu. Kumeneko angelo ndi maulamuliro ndi zimphamvu zimamvera Iye. Tsono popeza kuti Khristu adamva zoŵaŵa m'thupi mwake, valani dzilimbe ndi maganizo omwewo, chifukwa munthu amene wamva zoŵaŵa m'thupi mwake, ndiye kuti walekana nawo machimo. Choncho, pa nthaŵi yatsala yoti mukhale pansi pano, simudzatsatanso zilakolako za anthu, koma mudzatsata kufuna kwa Mulungu. Paja kale mudakhala mukutaya nthaŵi yochuluka pakuchita zinthu zimene akunja amazikonda. Munkatsata zonyansa, zilakolako zoipa, kuledzera, dyera, maphokoso apamoŵa, ndi kupembedza mafano konyansa. Anthu akunja amadabwa tsopano poona kuti mwaleka kuthamangira nao zoipitsitsa zimene iwo amachita mosadziletsa konse. Nchifukwa chake amalalata. Koma iwo adzayenera kufotokoza okha mlandu wao kwa Mulungu amene ali wokonzeka kuweruza amoyo ndi akufa. Nchifukwa chake Uthenga Wabwino udalalikidwa ndi kwa amene adafa omwe, kuti ngakhale adaweruzidwa m'thupi monga anthu, komabe mu mzimu akhale ndi moyo monga Mulungu. Chimalizo cha zonse chayandikira. Nchifukwa chake khalani ochenjera ndi odziletsa, kuti muthe kupemphera. Chachikulu nchakuti muzikondana mosafookera, popeza kuti chikondi chimaphimba machimo ochuluka. Poyenderana, muzisamalirana bwino mosadandaula. Aliyense mphatso imene adalandira kwa Mulungu azitumikira nayo anzake. Mukhale ngati akapitao ogwiritsa bwino ntchito mphatso zamitundumitundu zochokera kwa Mulungu. Aliyense amene amalankhula, mau ake akhaledi mau ochokera kwa Mulungu. Aliyense amene amatumikira, atumikire ndi mphamvu zimene Mulungu ampatsa, kuti pa zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu. Ulemerero ndi mphamvu ndi zake mpaka muyaya. Amen. Inu okondedwa, musazizwe ndi chimoto cha masautso chimene chakugwerani kuti muyesedwe nacho. Musaganize kuti zimene zakuwonekeranizo nzachilendo. Koma kondwerani popeza kuti mulikumva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, kuti podzaoneka ulemerero wake, mudzasangalale kwakukulu. Anthu akakuchitani chipongwe chifukwa cha dzina la Khristu, ndinu odala, chifukwa ndiye kuti Mzimu wa ulemerero, Mzimu wa Mulungu, wakhazikika pa inu. Pakati panu pasakhale ndi mmodzi yemwe wogwa m'mavuto chifukwa choti wapha munthu, kapena waba, kapena wachita choipa, kapena waloŵerera za eniake. Koma ngati mumva zoŵaŵa chifukwa chakuti ndinu akhristu, musachite manyazi, koma mulemekeze Mulungu chifukwa cha dzinalo. Nthaŵi ndiye yafika yoti Mulungu ayambe kuweruza anthu ake. Tsono ngati chiweruzocho chiyambira pa ife, nanga podzafika pa osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu, ndiye kuti chidzakhala chotani? Paja mau a Mulungu akuti, “Ngati wolungama yemwe adzapulumuka movutikira, nanga munthu wochimwa, wonyozera za Mulungu, adzatani?” Nchifukwa chake anthu amene amamva zoŵaŵa monga Mulungu afunira, adzipereke m'manja mwa Mlengi wao wokhulupirika, ndi kumachitabe ntchito zabwino. Tsopano ndili nawo mau akulu a mpingo amene ali pakati panu, ine mkulu mnzao. Ndinenso mboni ya zoŵaŵa za Khristu, ndipo ndikuyembekeza kudzalandira nao ulemerero umene uti udzaoneke. Mau angawo ndi aŵa: Ŵetani gulu la nkhosa za Mulungu zimene zili m'manja mwanu. Musaziyang'anire ngati kuti wina akuchita kukuumirizani, koma mofuna nokha, monga momwe afunira Mulungu. Musagwire ntchito yanuyo potsatira phindu lochititsa manyazi, koma ndi mtima wofunitsitsa kutumikira. Musakhale ngati mafumu odzikuza potsogolera anthu amene muyenera kuŵayang'anira, koma onetsani chitsanzo chabwino kwa nkhosazo. Ndipo pamene Mbusa wamkulu adzaonekera, mudzalandira mphotho yosafota yaulemerero. Inunso anyamata, muzimvera akulu. Ndipo nonsenu, khalani okonzeka kutumikirana modzichepetsa. Paja mau a Mulungu akuti. “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma amaŵakomera mtima anthu odzichepetsa.” Nchifukwa chake mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti pa nthaŵi yake adzakukwezeni. Tulani pa Iye nkhaŵa zanu zonse, popeza kuti Iye ndiye amakusamalirani. Khalani odziletsa, khalani maso. Mdani wanu Satana amakhala akuyenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, kufunafuna woti amudye. Mulimbane naye mutakhazikika m'chikhulupiriro, podziŵa kuti akhristu anzanu pa dziko lonse lapansi nawonso alikumva zoŵaŵa zomwezi. Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha. Iye ndiye mwini mphamvu mpaka muyaya. Amen. Kalatayi ndalembetsa Silivano mwachidule. Ndimamuwona kuti ndi mbale wokhulupirika. Ndafuna kukulimbitsani mtima, ndi kuchita umboni wakuti kukoma mtima kwenikweni kwa Mulungu nkumeneku. Chifukwa cha kukoma mtimako, limbikani. Anzanu a mu mpingo wa ku Babiloni akuti moni. Marko, mwana wanga, nayenso akuti moni. Mupatsane moni mwachikondi. Mtendere ukhale ndi inu nonse amene muli ake a Khristu. Ndine, Simoni Petro, mtumiki ndi mtumwi wa Yesu Khristu. Ndikulemba kalatayi kwa anthu amene adalandira chikhulupiriro chomwe ifenso tidalandirako. Iwonso adachilandira chifukwa cha chilungamo cha Mulungu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu. Mulungu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere wochuluka, pakumdziŵa Iyeyo ndiponso Yesu Ambuye athu. Mulungu mwa mphamvu zake adatipatsa zonse zotithandiza kukhala ndi moyo ndiponso opembedza, pakutidziŵitsa za Iyeyo amene adatiitana ku ulemerero ndi ubwino wake woposa. Mwa ulemerero ndi ubwino wakewo adatipatsa madalitso aakulu ndi amtengowapatali amene Iye adatilonjeza. Adatero kuti mulandireko moyo wake wa Mulungu, mutapulumuka ku chivunde chimene chili pa dziko lapansi chifukwa cha zilakolako zoipa. Tsono muyesetse kuchita khama kuwonjezera makhalidwe abwino pa chikhulupiriro chanu, ndi nzeru zoona pa makhalidwe anu abwinowo. Muwonjezerepo kudziletsa pa nzeru zoonazo, kulimbika pa kudziletsa kwanu, ndiponso kupembedza Mulungu pa kulimbika kwanuko. Pa kupembedzapo muwonjezerepo chifundo chachibale, ndipo pa chifundo chachibalecho muwonjezepo chikondi. Ngati zonsezi zikhala mwa inu, nkumachuluka, simudzakhala olephera ndi opanda phindu pa nzeru zodziŵira Ambuye athu Yesu Khristu. Paja munthu wopanda zimenezi ndiye kuti ngwakhungu, sangathe kuwona patali, ndipo waiŵala kuti adamtsuka machimo ake akale. Nchifukwa chake abale, chitani changu koposa kale kutsimikiza kuti Mulungu adakuitanani ndipo adakusankhani. Mukatero simudzagwa konse. Choncho adzakutsekulirani kwathunthu khomo loloŵera mu Ufumu wosatha wa Ambuye athu ndi Mpulumutsi wathu, Yesu Khristu. Nchifukwa chake cholinga changa nchakuti ndizikukumbutsani zimenezi nthaŵi zonse, ngakhale mukuzidziŵa ndipo mumakhulupirira ndi mtima wonse choona chimene mudalandira. Ndiyesa nkoyenera kuti, ndikadali mu msasa uno, nditsitsimutse mitima yanu pakukukumbutsani zimenezi. Pakuti ndikudziŵa kuti nthaŵi yakutuluka mu msasa wanga uno yayandikira, monga andidziŵitsira Ambuye athu Yesu Khristu. Ndipo ndidzayesetsa kukonza zoti nditachoka ine, muzidzatha kuzikumbukira zimenezi nthaŵi iliyonse. Ife sitidatsate nthano zongopeka chabe, pamene tidakudziŵitsani za mphamvu zao ndi za kubweranso kwao kwa Ambuye athu Yesu Khristu. Koma tidachita kuuwona ndi maso athu ukulu wake. Iye adalandira ulemu ndi ulemerero kwa Mulungu Atate, ndipo adamufikira mau ochokera kwa Atate aulemererowo akuti, “Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.” Ndipo mau ameneŵa ifeifeyo tidaŵamva kuchokera kumwamba chifukwa tidaali naye pamodzi pa phiri loyera lija. Motero tikudziŵa ndithu tsopano kuti mau aja a anereriŵa ngoona. Nkwabwino tsono kuti muŵayang'anitsitse ngati nyale yoŵala m'malo amdima, kufikira nthaŵi imene kudzayambe kucha, pamene nyenyezi yam'mamaŵa idzayambe kuŵala m'mitima mwanu. Koma choyamba mumvetse kuti munthu payekha sangathe kumasulira mau a aneneri olembedwa m'Malembo. Paja mau a aneneri sadadze konse ndi kufuna kwa munthu yekha, koma Mzimu Woyera adaŵalankhulitsa mau ochokera kwa Mulungu. Komabe panali aneneri ena onama ngakhale pakati pa Aisraele omwe. Momwemonso pakati pa inu padzaoneka aphunzitsi onama. Iwowo adzaloŵetsa mwachinsinsi zophunzitsa zonama ndi zoononga, ngakhale kukana kumene Mbuye wao amene adaŵaombola, ndipo motero adzadziitanira chiwonongeko mwamsanga. Ambiri adzatsata mkhalidwe wodzilekerera ndipo anthu adzanyoza njira ya choona chifukwa cha iwowo. Chifukwa chokondetsa chuma, iwo adzayesa kupeza phindu pakukuuzani mau onyenga. Komatu chilango chao nchokonzeratu kale, ndipo chiwonongeko chao chikuŵadikira. Pakuti Mulungu sadaŵalekerere angelo amene adachimwa aja, koma adaŵaponya m'ng'anjo yamoto, m'maenje amdima momwe ali omangidwa kudikira chiweruzo. Mulungu sadaŵalekererenso anthu akale aja, koma adangosunga Nowa yekha, mlaliki wa chilungamo, pamodzi ndi anzake asanu ndi aŵiri, pamene adadzetsa chigumula pa dziko la anthu osasamala za Iye Mulunguyo. Ndiponso Mulungu adaweruza mzinda wa Sodomu ndi wa Gomora naiwononga ndi moto, kuti chimenechi chikhale chitsanzo chochenjeza anthu amene adzakhale osasamala za Mulungu. Koma adapulumutsa Loti munthu wolungama, amene ankavutika ndi makhalidwe odzilekerera a anthu ochimwa aja. Munthu wolungama uja, pokhala pakati pao, analikumva ndi kuwona machitidwe ao oipa, ndipo tsiku ndi tsiku mtima wake wolungama unkavutikadi. Ndiye kuti pamene anthu osamala za Mulungu akuyesedwa, Iye amadziŵa kuŵapulumutsa kwake. Koma amadziŵanso kusunga osalungama kuti alangidwe mpaka tsiku la chiweruzo. Makamaka adzalanga anthu amene amatsata zilakolako zonyansa zathupi namanyoza ulamuliro. Aphunzitsi onyenga ndi odzikuza, osasamala munthu, saopa kuchita chipongwe aulemerero a Kumwamba. Chonsecho ngakhale angelo, amene ali aakulu ndi amphamvu kuposa aphunzitsi onyengaŵa, sanyazitsa aulemererowo pamaso pa Ambuye. Koma anthu aŵa ali ngati nyama chabe, zolengedwa zopanda nzeru, zobadwira kuti zizigwidwa ndi kumaphedwa. Amanyoza mwachipongwe zinthu zosazidziŵa. Ndipo monga nyama zija, iwo omwe adzaonongedwa, nadzalangidwa molingana ndi kuipa kwao. Chimene chimaŵakomera nkumangochita zokondweretsa thupi nthaŵi yamasana. Ali ngati mathotho ndi maŵanga onyansa, chifukwa podya nanu pamodzi amakondwera kuchita zonyenga. Maso ao ndi adama, osafuna kuleka kuchimwa. Amanyengerera anthu a mtima wosakhazikika. Ali ndi mtima wozoloŵera kuumirira chuma. Anthu otembereredwa! Adasiya njira yolungama, adasokera potsata njira ya Balamu, mwana wa Beori, amene ankafunitsa kupata mphotho pochita zosalungama. Koma adadzudzulidwa chifukwa cha kulakwa kwakeko. Bulu, nyama yosalankhula, adalankhula ngati munthu, kuletsa zamisala za mneneriyo. Aphunzitsi onyengaŵa ali ngati akasupe opanda madzi, ngati nkhungu yokankhidwa ndi mphepo yamkuntho. Mulungu adaŵasungira mdima wakuda wabii. Iwowotu amalankhula mau odzitama auchitsiru, ndipo ndi zilakolako zonyansa zathupi amanyengerera anthu amene angopulumuka chatsopano pakati pa anzao oipa. Amaŵalonjeza ufulu, chonsecho eniakewo ndi akapolo a chivunde. Pajatu munthu amasanduka kapolo wa chimene chamugonjetsa. Chifukwatu ngati anthu apulumuka ku zodetsa za dziko lino lapansi, pakudziŵa Ambuye athu ndi Mpulumutsi wathu, Yesu Khristu, pambuyo pake nkugwidwanso ndi kugonjetsedwa ndi zoipa zomwezo, potsiriza adzakhala oipa koposa m'mene analiri poyamba. Kukadakhala bwino kwa iwo akadakhala osadziŵa njira ya chilungamo, koposa kuileka atadziŵa lamulo loyera limene Mulungu adaŵapatsa. Pakutero akutsimikiza kuti ngwoona mwambi uja wakuti, “Galu wabwerera ku masanzi ake,” ndi wina ujanso wakuti, “Nkhumba imene inasamba, yakunkhuliranso m'matope.” Inu okondedwa, kalata ndikukulemberaniyi ndi yachiŵiri. M'makalata aŵiri onseŵa ndafuna kuutsa mitima yanu kuti mukhale ndi maganizo oona. Kumbukirani mau amene aneneri oyera adanena kale, ndiponso lamulo la Ambuye ndi Mpulumutsi wathu limene atumwi adakupatsani. Choyamba mumvetse izi: pa masiku otsiriza kudzafika anthu olalata, otsata zilakolako zao zoipa. Azidzalalata nkumanena kuti, “Kodi suja Ambuye adalonjeza kuti adzabweranso? Nanga ali kuti? Lija nkale adamwalira makolo athu, koma zonse zili monga momwe Mulungu adazilengera poyamba paja.” Apa akuiŵala dala kuti kalelo Mulungu atanena mau, zakuthambo zidalengedwa, ndipo dziko lapansi lidapangidwa ndi madzi kufumira m'madzi. Ndipo ndi madzi okhaokhawo dziko lapansi la masiku amenewo lidamizidwa ndi kuwonongedwa. Koma Mulungu ndi mau omwe aja adasunga zakuthambo ndi dziko lapansi la masiku ano kuti adzazitenthe ndi moto. Akuzisunga kufikira tsiku limene adzaweruza ndi kuwononga anthu onse osasamala za Iye. Koma inu okondedwa, chinthu chimodzi musaiŵale, kuti pamaso pa Ambuye tsiku limodzi lili ngati zaka chikwi chimodzi, ndipo zaka chikwi chimodzi zili ngati tsiku limodzi. Sikuti akuzengereza kuchita zimene adalonjeza, monga m'mene ena amaganizira, koma akukulezerani mtima. Safuna kuti ena aonongedwe, koma afuna kuti onse atembenuke mtima. Koma tsiku la Ambuye lidzafika ngati mbala. Pa tsikulo zakumwamba zidzatha ndi phokoso loopsa. Zinthu zonse zidzayaka moto nkusungunuka, ndipo dziko lapansi ndi zonse zili m'menemo zidzapseratu. Popeza kuti zonsezi zidzasungunuka motero, nanga simuyenera kukhala anthu angwiro m'makhalidwe anu ndiponso osamala za Mulungu? Muziyembekeza tsiku la Ambuye ndi kugwira ntchito zofulumizitsa kudza kwake. Pa tsikulo zakumwamba zidzayaka moto ndi kusungunuka, ndipo zinthu zonse nazonso zidzasungunukira m'motomo. Koma potsata lonjezo la Mulungu, tikudikira kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano, m'mene chilungamo chizidzakhalamo. Choncho inu okondedwa, popeza kuti mukudikira zimenezi, muzichita changu kuti Ambuye adzakupezeni muli opanda banga kapena chilema ndiponso muli pa mtendere ndi Ambuyewo. Zindikirani kuti Ambuye athu akukulezerani mtima kuti mupulumuke. Paulo, mbale wathu wokondedwa uja, nayenso adakulemberani za zimenezi ndi nzeru zimene Mulungu adampatsa. Paja amanena chimodzimodzi m'makalata ake onse polemba za zimenezi. M'makalatamo muli zina zapatali kuzimvetsa, ndipo anthu osaphunzira ndi a nzeru zosakhazikika amazipotoza, monga amapotozeranso Malembo ena. Pakutero akungodziwononga okha. Tsono inu okondedwa, popeza kuti mwazidziŵiratu zimenezi, chenjerani kuti zolakwa za anthu ochimwa zingakusokeretseni ndipo mungagwedezeke kenaka nkugwa. Koma mukule m'chifundo ndi m'nzeru za Yesu Khristu, Ambuye athu ndi Mpulumutsi wathu. Iye akhale ndi ulemerero tsopano ndi mpaka muyaya. Amen. Tikukulemberani za Iye uja amene adaalipo kuyambira pa chiyambi, amene tidamumva ndipo tidamuwona ndi maso athu, amene tidampenya ndithu, ndipo tidamkhudza ndi manja athu: Iyeyo ndiye Mau opatsa moyo. Moyowo udaoneka, ndipo ife tidauwona. Tikuuchitira umboni, ndipo tikukulalikirani za moyo wosatha, umene unali kwa Atate ndipo udatiwonekera. Chimene tidachiwona ndi kuchimva, tikukulalikirani, kuti inunso mukhale a mtima umodzi ndi ife. Kuyanjana kwathu tikuyanjana ndi Atate, ndiponso ndi Mwana wao, Yesu Khristu. Tikukulemberani zimenezi kuti chimwemwe chathu chikhale chathunthu. Uthenga umene tidamva kwa Iye, ndipo timaulalika kwa inu, ndi wakuti Mulungu ndiye kuŵala, ndipo mwa Iye mulibe mdima konse. Tikanena kuti timayanjana naye, pamene tikuyendabe mu mdima, tikunama, ndipo zochita zathu nzosagwirizana ndi zoona. Koma tikamayenda m'kuŵala, monga Iye ali m'kuŵala, pamenepo tikuyanjana tonsefe. Ndipo magazi a Yesu, Mwana wake, amatitsuka ndi kutichotsera tchimo lililonse. Tikanena kuti tilibe tchimo, tikudzinyenga, ndipo mwa ife mulibe choona. Koma tikamavomera kuti ndife ochimwa, Mulungu amene ali wokhulupirika ndi wolungama, adzatikhululukira machimo athuwo. Adzatiyeretsa ndi kutichotsera kusalungama kwathu konse. Tikanena kuti sitidachimwe, tikumuyesa wonama Mulungu, ndipo mau ake sali mwa ife. Inu ana anga, ndikukulemberani zimenezi kuti musamachimwa. Komabe wina akachimwa, tili nayo Nkhoswe yotinenera kwa Atate, ndiye Yesu Khristu amene ali wolungama. Iyeyo ndiye nsembe yopepesera machimo athu, ndipo osati athu okha, komanso a anthu a pa dziko lonse lapansi. Pakutsata malamulo a Mulungu, ndi pamene tingatsimikize kuti timamdziŵa. Munthu akamati, “Ine ndimadziŵa Mulungu”, koma chikhalirecho satsata malamulo ake, angonama ameneyo, ndipo mwa iye mulibe choona. Koma munthu akamasunga mau a Mulungu, pamenepo chikondi cha Mulungu chafikadi pake penipeni mwa iyeyo. Chotitsimikizitsa kuti tili mwa Iye, ndi chimenechi. Munthu akamati amakhala mwa Mulungu, zochita zake zizilingana ndi zimene Yesu ankachita. Inu okondedwa, sindikukulemberani lamulo latsopano, koma lakale lomwe lija, limene mwakhala nalo kuyambira pa chiyambi. Lamulo lakalelo ndi mau amene mudaŵamva kale. Komabe ndi lamulo latsopano limene ndikukulemberani. Zimene lamuloli likunena, zidachitikadi mwa Yesu, ndipo zikuchitikanso mwa inu. Pajatu mdima ulikutha, ndipo kuŵala kwenikweni kwayamba kale kuti ngwee. Munthu akamati ali m'kuŵala, komabe nkumadana ndi mnzake, akali mu mdima ameneyo. Koma munthu wokonda mnzake, amakhala m'kuŵala, ndipo mwa iye mulibe chokhumudwitsa. Munthu wodana ndi mnzake, ali mu mdima, ndipo akuyenda mu mdima. Sadziŵa kumene akupita, chifukwa mdima wamudetsa m'maso. Inu ana, ndikukulemberani popeza kuti Mulungu wakukhululukirani machimo anu chifukwa cha dzina la Khristu. Inu atate, ndikukulemberani, chifukwa mumamdziŵa Iye amene alipo kuyambira pa chiyambi. Inu achinyamata, ndikukulemberani, chifukwa mwampambana Woipa uja. Ndimakulemberani inu ana, chifukwa Atate mumaŵadziŵa. Ndimakulemberani inu atate, chifukwa mumamdziŵa Iye amene alipo kuyambira pa chiyambi. Ndimakulemberani inu achinyamata, chifukwa ndinu amphamvu, mau a Mulungu amakhala mwa inu, ndipo mwampambana Woipa uja. Musamalikonde dziko lapansi kapena zinthu zapansipano. Munthu akamakonda dziko lapansi, chikondi chokonda Atate sichikhalamo mwa iye. Paja zonse zapansipano, zilakolako zathupi, zinthu zimene maso amakhumbira, ndiponso kunyadira za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku mkhalidwe woipa wa dziko lapansi. Ndipotu dziko lapansi likupita, pamodzi ndi zake zonse zimene anthu amazilakalaka. Koma munthu wochita zimene Mulungu afuna, amakhalapo mpaka muyaya. Ananu, ino ndi nthaŵi yotsiriza. Mudamva kuti kukubwera Woukira Khristu, ndipo tsopano aoneka kale ambiri oukira Khristu. Zimenezi zikutizindikiritsa kuti ino ndi nthaŵi yotsirizadi. Anthuwo adachita kuchoka pakati pathu, komabe sanali a gulu lathu kwenikweni. Pakuti akadakhala a gulu lathu, bwenzi akali nafebe. Koma adatichokera, kuti aonekere poyera kuti panalibe ndi mmodzi yemwe mwa iwo amene anali wa gulu lathu. Koma inuyo, mudadzozedwa ndi Woyera uja, ndipo nonse mukudziŵa. Ndakulemberani, osati chifukwa chakuti simudziŵa choona, koma chifukwa chakuti mumachidziŵa, ndipo mukudziŵanso kuti bodza silichokera ku choona. Wabodzayo ndani? Kodi si amene amanena kuti Yesu si Mpulumutsi wolonjezedwa uja? Wokana Atate ndi Mwana, ameneyo ndiye Woukira Khristu. Aliyense wokana Mwana, alibenso Atate. Wovomereza Mwana, alinso ndi Atate. Koma inu, zimene mudamva kuyambira pa chiyambi, zikhalebe m'mitima mwanu. Zimene mudamva kuyambira pa chiyambi zikakhalabe m'mitima mwanu, inunso mudzakhala mwa Mwana ndi mwa Atate. Ndipo chimene adalonjeza nchimenechi: moyo wosatha. Ndikukulemberani zimenezi kuti ndikuuzeni za iwo aja amene amafuna kukusokeretsani. Koma inu, Khristu adakudzozani ndi Mzimu Woyera amene amakhala mwa inu, ndipo sipafunikanso wina woti akuphunzitseni. Mzimu Woyerayo, amene mudadzozedwa naye, amakuphunzitsani zonse. Zimene amakuphunzitsani nzoona, si zonama ai. Nchifukwa chake, monga momwe adakuphunzitsirani, khalani mwa Khristu. Tsono ananu, khalani mwa Iye, kuti tikakhale olimba mtima Iye akadzaoneka, ndipo tisadzachite manyazi Iye akadzabweranso. Ngati mukudziŵa kuti Khristu ndi wolungama, musapeneke konse kuti aliyense wochita chilungamo, ndi mwana wa Mulungu. Onani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate adatikonda nacho. Adatikonda kwambiri, kotero kuti timatchedwa ana a Mulungu. Ndipo ndifedi ana ake. Anthu odalira zapansipano satidziŵa ifeyo, chifukwa Iyeyonso sadamdziŵe. Inu okondedwa, ndife ana a Mulungu tsopano. Mulungu sadatiwonetsebe chimene tidzakhale. Koma tikudziŵa kuti Iye akadzaoneka, tidzakhala ofanafana naye, pakuti tidzamuwona monga momwe aliri. Munthu aliyense amene ali ndi chiyembekezo chimenechi pa Khristu, amadzisandutsa woyera monga momwe Khristuyo ali woyera. Aliyense amene amachimwa, alinso ndi mlandu wa kuphwanya malamulo. Paja kuchimwa nkuphwanya malamulo kumene. Mukudziŵa kuti Khristu adaoneka kuti adzachotse machimo, ndipo mwa Iye mulibe tchimo. Munthu aliyense wokhala mwa Khristu, sachimwa. Aliyense amene amachimwa, sadamuwone ndipo sadamdziŵe. Ana anga, wina aliyense asakusokeretseni. Munthu amene amachita chilungamo, ngwolungama monga Khristu ali wolungama. Munthu amene amachimwa, ndi wa Satana, pakuti Satana ndi wochimwa kuyambira pa chiyambi. Mwana wa Mulungu adaoneka ndi cholinga chakuti aononge zochita za Satana. Aliyense amene ali mwana wa Mulungu, sachimwirachimwira, popeza kuti umulungu wake wa Mulunguyo uli mwa iye. Sangathe kumachimwirachimwira, chifukwa ndi mwana wa Mulungu. Kusiyana kwake pakati pa ana a Mulungu ndi ana a Satana kumaoneka motere: aliyense wosachita chilungamo, ndiponso wosakonda mnzake, sali mwana wa Mulungu. Uthenga umene mudamva kuyambira pa chiyambi ndi wakuti tizikondana. Tisakhale ngati Kaini amene anali wake wa Woipa uja, ndipo adapha mbale wake. Chomuphera chinali chiyani? Chifukwa zochita zake zinali zoipa, koma za mbale wake zinali zolungama. Motero musadabwe abale, anthu odalira zapansipano akamadana nanu. Ife tikudziŵa kuti mu imfa tidatulukamo nkuloŵa m'moyo, popeza kuti timakonda anzathu. Munthu amene sakonda mnzake, akali mu imfa. Aliyense wodana ndi mnzake, ndi wopha anthu. Ndipo mukudziŵa kuti aliyense wopha anthu, alibe moyo wosatha mumtima mwake. Tazindikira chikondi tsopano pakuwona kuti Khristu adapereka moyo wake chifukwa cha ife. Choncho ifenso tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale athu. Koma munthu akakhala ndi chuma, ndipo aona mnzake ali wosoŵa, iye nkumuumira mtima namumana, kodi chikondi cha Mulungu chingakhalemo bwanji mumtima mwake? Ananu, chikondi chathu chisamangokhala cha nkhambakamwa chabe, koma chiziwoneka pa zochita zathu. Apo tidzadziŵa kuti tili pa choona, ndipo tidzakhala okhazika mtima pamaso pa Mulungu nthaŵi zonse pamene mtima wathu ukutitsutsa kuti ndife olakwa. Paja Mulungu ndi wamkulu kopambana mtima wathu, ndipo amadziŵa zonse. Inu okondedwa, ngati mtima wathu sutitsutsa, titha kuima mopanda mantha pamaso pa Mulungu. Ndipo chilichonse chimene timpempha, amatipatsa, chifukwa timatsata malamulo ake, ndipo timachita zomkondweretsa. Chimene Mulungu amalamula nchakuti tizikhulupirira Mwana wake Yesu Khristu, ndipo kuti tizikondana monga Iye adatilamulira. Munthu wotsata malamulo a Mulungu, amakhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu amakhala mwa iye. Chifukwa cha Mzimu Woyera amene adatipatsa, timadziŵa kuti Mulungu amakhaladi mwa ife. Inu okondedwa, musamakhulupirira maganizo aliwonse, koma muziŵayesa maganizowo kuti muwone ngati ndi ochokeradi kwa Mulungu. Paja aneneri ambiri onama awanda ponseponse. Mungathe kuzindikira Mzimu wa Mulungu motere: aliyense wovomereza kuti Yesu Khristu adadzakhaladi munthu, ameneyo ndi wochokera kwa Mulungu. Koma aliyense wosavomereza Yesu, ameneyo ndi wosachokera kwa Mulungu. Maganizo akewo ndi ochokera kwa Woukira Khristu, yemwe uja mudamva kuti akubwerayu; ndipotu wafika kale m'dziko lapansi. Koma inu, ana anga, ndinu ake a Mulungu, ndipo mwaŵapambana aneneri onamawo. Pakuti Iye amene ali mwa inu, ndi wopambana iye uja amene ali mwa anthu odalira zapansipano. Aneneri onamawo ndi apansipano, nchifukwa chake zimene amalankhula nzapansipano, ndipo anthu odalira zapansipano amaŵamvera. Koma ife ndife ake a Mulungu. Munthu wodziŵa Mulungu, amatimvera. Koma iye amene sali wake wa Mulungu, satimvera. Umu ndi m'mene timasiyanitsira pakati pa maganizo oona ndi maganizo onama. Inu okondedwa, tizikondana, pakuti chikondi nchochokera kwa Mulungu. Aliyense amene ali ndi chikondi, ndi mwana wa Mulungu, ndipo amadziŵa Mulungu. Koma munthu wopanda chikondi sadziŵa Mulungu, pakuti Mulungu ndiye chikondi chimene. Mulungu adaonetsa chikondi chake kwa ife motere: Iye nkukhala ndi Mwana mmodzi yekha, koma adamtuma pansi pano, kuti mwa Iye tikhale ndi moyo. Chikondi chenicheni ndi ichi, chakuti sindife tidakonda Mulungu ai, koma Mulungu ndiye adatikonda ifeyo, natuma Mwana wake kuti akhale nsembe yopepesera machimo athu. Inu okondedwa, ngati Mulungu adatikonda kwambiri chotere, ifenso tiyenera kumakondana. Palibe munthu amene adaona Mulungu. Koma tikamakondana, Mulungu amakhala mwa ife, ndipo chikondi chake chafika pake penipeni mwa ife. Tikudziŵa kuti timakhala mwa Mulungu, ndipo Iyenso amakhala mwa ife, chifukwa adatipatsa Mzimu wake Woyera. Ife taona, ndipo tikuchita umboni, kuti Atate adatuma Mwana wake kuti adzakhale Mpulumutsi wa anthu a pa dziko lonse lapansi. Aliyense wovomereza kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu, Mulungu amakhala mwa iye, ndipo iye amakhala mwa Mulungu. Motero ife timadziŵa ndipo timakhulupirira ndithu kuti Mulungu amatikonda. Mulungu ndiye chikondi, ndipo munthu wokhala ndi moyo wachikondi, amakhala mwa Mulungu, Mulungunso amakhala mwa iye. Pamene chikondi chafikira pake penipeni mwa ife ndi apa pakuti moyo wathu pansi pano uli wonga moyo wa Khristu, kotero kuti tingathe kukhala olimba mtima pa tsiku la chiweruzo. Munthu amene ali ndi chikondi, alibe mantha, pakuti chikondi changwiro chimatulutsira mantha kunja. Munthu akamachita mantha, ndiye kuti akuwopa chilango, ndipo chikondi sichidafike pake penipeni mwa iye. Ife timakonda Mulungu chifukwa ndiye adayamba kutikonda. Wina akamanena kuti, “Ndimakonda Mulungu”, komabe nkumadana ndi mbale wake, ndi wonama ameneyo. Pakuti munthu wosakonda mbale wake amene wamuwona, sangathe kukonda Mulungu amene sadamuwone. Lamulo limene Iye adatipatsa ndi lakuti, wokonda Mulungu azikondanso mbale wake. Munthu aliyense wokhulupirira kuti Yesu ndi Mpulumutsi wolonjezedwa uja, iyeyo ndi mwana wa Mulungu. Ndipo aliyense wokonda nakubala, amakonda ndi mwana wake yemwe. Chodziŵira kuti timakonda ana a Mulungu nchakuti timakonda Mulungu ndi kutsata malamulo ake. Paja kukonda Mulungu ndiye kuti kutsata malamulo ake, ndipo malamulo ake si olemetsa. Chifukwa aliyense amene ali mwana wa Mulungu, amagonjetsa dziko lapansi. Chimene timagonjetsera dziko lapansilo ndi chikhulupiriro chathu. Ndani amagonjetsa dziko lapansi? Amaligonjetsa si wina ai, koma wokhulupirira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu. Yesu Khristu ndiye amene adabwera kudzera mwa madzi ndi mwa magazi. Sadabwere mwa madzi okha, koma mwa madzi ndi mwa magazi omwe. Ndipo Mzimu Woyera ndiye amene amachitirapo umboni, pakuti Mzimuyo ndiye choona. Motero pali atatu aŵa ochitira umboni: Mzimu Woyera, madzi ndi magazi, ndipo atatuŵa amavomerezana. Timalandira umboni wa anthu, koma umboni wa Mulungu ndi wopambana umboni wa anthu. Umboniwo ndi umene Mulungu adachitira Mwana wake. Amene amakhulupirira Mwana wa Mulungu, ali nawo umboniwo mumtima mwake. Amene sakhulupirira Mulungu, amayesa kuti Mulungu ndi wonama, chifukwa sakhulupirira umboni umene Mulungu adachitira Mwana wake. Umboniwo tsono ndi wakuti Mulungu adatipatsa moyo wosatha, ndipo moyowo umapezeka mwa Mwana wake. Amene ali ndi Mwanayo, ali nawo moyo. Amene sali ndi Mwana wa Mulungu, alibe moyo. Inu amene mumakhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu, ndakulemberani zimenezi kuti mudziŵe kuti muli ndi moyo wosatha. Ndipo timalimba mtima pamaso pa Mulungu, popeza kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse komukomera. Ndipo ngati tikudziŵa kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse, timadziŵanso kuti talandiradi zimene tampempha. Wina akaona mbale wake akuchita tchimo losadzetsa imfa, apemphere, ndipo Mulungu adzampatsa moyo mbale wakeyo. Ndikunenatu za ochita tchimo losadzetsa imfa. Koma lilipo tchimo lina lodzetsa imfa, za tchimo limenelo sindikunena kuti apemphere ai. Chinthu chilichonse chosalungama ndi tchimo, koma pali lina tchimo losadzetsa imfa. Tikudziŵa kuti aliyense amene ali mwana wa Mulungu, sachimwirachimwira. Yesu, Mwana wa Mulungu, amamsunga, ndipo Woipa uja sangamkhudze. Tikudziŵa kuti ndife ake a Mulungu, ndipo kuti onse odalira zapansipano ali m'manja mwa Woipa uja. Tikudziŵa kuti Mwana wa Mulungu adafika, ndipo adatipatsa nzeru kuti timdziŵe Mulungu woona. Ndipo tili mwa Mulungu woonayo, chifukwa tili mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iyeyo ndiye Mulungu woona ndiponso moyo wosatha. Ana inu, dzisungeni bwino, osapembedza mafano. Ine mkulune ndikulemba kalatayi kwa mai wosankhidwa ndi Mulungu, ndi kwa ana ake amene ndimaŵakonda kwenikweni. Ndipo sindine ndekha amene ndimakukondani, komanso onse odziŵa choona. Timakukondani chifukwa cha choona chimene chimakhala mwa ife, ndipo chidzakhala nafe mpaka muyaya. Mulungu Atate ndi Yesu Khristu, Mwana wa Atate, atikomere mtima ndi kutipatsa chifundo ndi mtendere m'choona ndi m'chikondi. Ndidakondwera kwambiri kuti ndidapeza ana anu ena akuyenda motsata choona, monga Atate adatilamulira. Ndiye tsopano ndikukupemphani mai: tizikondana. Pakutero sindikukulemberani lamulo latsopano ai, koma lomwe lija limene takhala nalo kuyambira pa chiyambi. Chikondi chimene ndikunenachi nchakuti tikhale omvera malamulo a Mulungu. Lamulo limene ndikukulemberanilo, monga mudamva kuyambira pa chiyambi, ndi lakuti moyo wanu uzikhala wachikondi. Paja pakuwoneka anthu ambiri onyenga pa dziko lapansi. Iwo savomereza kuti Yesu Khristu adadzakhaladi munthu. Munthu wosavomereza zimenezi ndi wonyenga, ndiponso woukira Khristu. Chenjerani kuti mungataye chimene mwagwirira ntchito, koma yesetsani kuti mukalandire mphotho yathunthu. Aliyense amene sasunga chiphunzitso cha Khristu, koma amaonjezerapo zina, alibe Mulungu. Koma amene amasunga chiphunzitsocho, ameneyo alinso ndi Atate ndi Mwana. Wina aliyense akadza kwa inu osaphunzitsa zimenezi, musamlandire m'nyumba mwanu. Musampatse ndi moni womwe, pakuti wopatsa munthu wotere moni, akuvomereza zochita zake zoipa. Ndili ndi zambiri zoti ndikuuzeni, koma sindifuna kuzilemba m'kalata. Ndikuyembekeza kubwera kwanuko kuti tidzakambirane pakamwa mpakamwa. Pamenepo chimwemwe chathu chidzakhala chathunthu. Ana a mbale wanu wosankhidwa ndi Mulungu akuti moni. Ine mkulune ndikulemba kalatayi kwa Gayo wokondedwa, amene ndimamkonda kwenikweni. Wokondedwa, ndimapemphera kuti zako zonse zikuyendere bwino, ndipo kuti moyo wako wathupi ukhale wolimba, monga momwe uliri moyo wako wauzimu. Ine ndidaakondwa kwambiri pamene abale ena adafika nkumafotokoza za moyo wako m'choona, ndiponso za m'mene umayendera motsata choona. Palibe chondikondweretsa kwambiri koposa kumva kuti ana anga akuyenda m'choona. Wokondedwa, umatsata chikhulupiriro chako pa zonse zimene umachitira abale, makamaka akakhala alendo. Iwo adachitira umboni chikondi chako pamaso pa mpingo. Ndi bwinodi kuti uŵathandize mokondweretsa Mulungu kupitiriza ulendo wao. Paja adaanyamuka ulendo wao chifukwa cha dzina la Khristu, osalandira thandizo kwa akunja. Tsono ife tiyenera kumaŵathandiza anthu otere, kuti tigwirizane nawo pa ntchito yofalitsa choona. Ndidalembera mpingo mau pang'ono, koma Diotrefe safuna kundimvera. Iye amafuna kukhala mtsogoleri. Choncho ndikabwera, ndidzakumbutsa ntchito zimene amachita. Iye amandilalatira ndi mau oipa. Ndipo sachita zokhazi ai, komanso iyeiyeyo amakana kulandira abale, ndipo anthu ofuna kuŵalandira, iye amaŵaletsa, nkumaŵatulutsa mu mpingo. Wokondedwa, usamatsanzire zoipa, koma zabwino. Aliyense wochita zabwino, ndi mwana wa Mulungu, koma wochita zoipa, sadaone Mulungu. Demetrio anthu onse amamchitira umboni wabwino. Ngakhale choona chomwe chimamchitira umboni. Ifenso tikumchitira umboni, ndipo iweyo ukudziŵa kuti umboni wathu ndi woona. Ndinali ndi zambiri zoti ndikuuze, koma sindingakonde kuzilemba m'kalata. Ndikuyembekeza kudzakuwona posachedwa. Pamenepo tidzakambirana pakamwa mpakamwa. Mtendere ukhale nawe. Abwenzi onse akuti moni. Uperekeko moni kwa abwenzi onse mmodzimmodzi. Ndine, Yuda, mtumiki wa Yesu Khristu, ndiponso mbale wa Yakobe. Ndikulemba kalatayi kwa inu amene Mulungu adakuitanani, amene Mulungu Atate athu amakukondani ndi kukusungani, kusungira Yesu Khristu. Mulungu achulukitse chifundo chake, mtendere wake ndi chikondi chake kwa inu. Inu okondedwa, ndinkafunitsitsa kukulemberani kalata, kuti ndikufotokozereni za chipulumutso chokhudza tonsefe. Ndiye mtima wanga udandikakamiza kuti ndikulembereni tsopano ndi kukupemphani kolimba, kuti mumenye ndithu nkhondo yotchinjiriza chikhulupiriro, chimene Mulungu adapatsa anthu ake kamodzi kokhako. Paja anthu ena osasamala za Mulungu adaloŵa mobisika pakati panu. Iwo amapotoza kukoma mtima kwa Mulungu, ndi kukuyesa ufulu wochitira zonyansa. Amakana Yesu Khristu, amene Iye yekha ndiye Mbuye wathu ndi Mfumu yathu. Zakuti anthu ameneŵa adzalangidwa zidalembedwa kale lomwe. Tsopano ndati ndikukumbutseni zina, ngakhale mudazidziŵa kale zonse. Paja Ambuye adaapulumutsa mtundu wa Aisraele ku dziko la Ejipito, koma pambuyo pake adaŵaononga onse amene sadakhulupirire. Mukumbukire angelo amene sadakhutire ndi ulamuliro wao, koma adasiya malo amene Mulungu adaaŵapatsa. Mulungu adaŵamanga ndi maunyolo osatha, ndipo akuŵasunga m'malo amdima mpaka tsiku lalikulu lija pamene adzaŵaweruza. Mukumbukirenso mizinda ya Sodomu ndi Gomora ija, ndi mizinda yoyandikana nayo. Anthu ake m'menemonso ankangochita dama, namachitanso zonyansa zotsutsana ndi umunthu. Mulungu adaaŵaika ngati chitsanzo pakuŵalanga ndi moto wosatha. Komabe anthu ameneŵa akuchita chimodzimodzi. Potsata maloto ao, amaipitsa matupi ao, amakana ulamuliro wa Mulungu, ndipo amachita chipongwe aulemerero a Kumwamba. Koma ngakhale Mikaele yemwe, mkulu wa angelo, pamene iye ankakangana ndi Satana ndi kutsutsana naye za mtembo wa Mose, sadafune kutchuliliza mwachipongwe kuti ndi wolakwa. Adangoti, “Ambuye akulange!” Koma anthu ameneŵa amachita chipongwe zinthu zimene sazidziŵa. Ndipo zinthu zimene amazidziŵa ndi nzeru zachibadwa, zonga za nyama, ndizo zimene zimaŵaononga. Iwoŵa ali ndi tsoka, chifukwa adatsata njira ya Kaini. Monga adaachitira Balamu, iwonso adagwa m'cholakwa chifukwa chotsata phindu la ndalama. Adaonongeka chifukwa cha kuukira Mulungu, monga adaachitira Kora. Ameneŵa ndiwo amaipitsa maphwando anu achikondi. Amadya nanu mochitisa manyazi, nangosamala za iwo okha. Ali ngati mitambo youluzika ndi mphepo, koma osadzetsa mvula. Ali ngati mitengo yosabala zipatso ngakhale pa nyengo yake, imene idaferatu ndipo anthu adaizula. Ali ngati mafunde aukali apanyanja, amene amatulutsa thovu la zonyansa zao. Ali ngati nyenyezi zosokera, ndipo Mulungu akuŵasungira mdima wandiweyani mpaka muyaya. Mbiri iyi idadziŵika pakati pa Aisraele, koma siinalembedwe m'Chipangano Chakale. Enoki, wa mbadwo wachisanu ndi chiŵiri kuyambira pa Adamu, adaalosa za anthu okhaokhaŵa pamene adati, “Onani, Ambuye akubwera ndi angelo ake osaŵerengeka, kuti adzaweruze anthu onse. Adzagamula kuti ngolakwa onse osasamala za Mulungu, chifukwa cha ntchito zao zonse zosalungama, zimene adachita mosaopa Mulungu. Adzaŵatsutsa chifukwa cha mau onse achipongwe amene iwo, anthu ochimwa ndi onyozera za Mulungu, adanyoza nawo Ambuye.” Anthu ake ndi aŵa: ong'ung'udza, odandaula, ndi omangotsata zilakolako zao zoipa. Amalankhula zonyada, ndipo amangotamanda anthu moshashalika chifukwa chofuna kupezerapo phindu. Koma inu okondedwa, muzikumbukira mau amene atumwi a Ambuye athu Yesu Khristu adaneneratu. Paja adakuuzani kuti, “Pa masiku otsiriza kudzafika anthu onyoza, otsata zilakolako zao zoipa.” Anthu ameneŵa ndi oyambitsa mipatuko. Amangotsata zapansipano, ndipo mumtima mwao alibe Mzimu Woyera. Koma inu okondedwa, muzithandizana kuti uzikulirakulira moyo wanu, umene udakhazikika pa maziko a chikhulupiriro chanu changwiro. Muzipemphera ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Mudzisunge m'chikondi cha Mulungu podikira moyo wosatha, umene Ambuye athu Yesu Khristu adzakupatseni mwa chifundo chake. Pali ena amene ali okayika, amenewo muziŵachitira chifundo. Koma ena muŵapulumutse pakuŵalanditsa ku moto. Enanso muŵachitire chifundo, koma mwamantha, muzidana ngakhale ndi chovala chao chomwe choipitsidwa ndi machimo. Akhale ndi ulemerero Iye amene angathe kukusungani kuti mungagwe m'machimo, amene angathenso kukufikitsani pamaso pa ulemerero wake, muli okondwa ndi opanda chilema konse. Mulungu, amene Iye yekha ndiye Mpulumutsi wathu mwa Yesu Khristu Ambuye athu, akhale ndi ulemerero, ukulu, mphamvu ndi ulamuliro, isanayambe nthaŵi, tsopano, ndi mpaka muyaya. Amen. Buku lino likufotokoza zimene Yesu Khristu adaulula. Mulungu adampatsa zimenezi kuti aonetse atumiki a Mulunguyo zomwe zikuyenera kudzachitika posachedwa. Khristu pofuna kudziŵitsa zinthuzo mtumiki wake Yohane, adachita kutuma mngelo wake kwa iye. Yohaneyo wafotokoza zonse zimene adaziwona, ndipo wachitira umboni mau a Mulungu, ndiponso zonse zimene Yesu Khristu adanena. Ngwodala munthu amene aŵerenga momveka mauŵa. Ngodalanso anthu amene amvera mau a m'buku limeneli loneneratu zam'tsogolo, ndi kutsata zimene zalembedwamo. Pakuti nthaŵi yoti zichitike zonsezi ili pafupi. Ndine, Yohane, ndikulembera mipingo isanu ndi iŵiri ya ku Asiya. Akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere Mulungu amene alipo, amene analipo kale, amene alikudza. Ikukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere mizimu isanu ndi iŵiri yokhala patsogolo pa mpando wachifumu wa Mulungu. Akukomereninso mtima ndi kukupatsani mtendere Yesu Khristu, mboni yokhulupirika, amene ali woyambirira kulandira moyo waulemerero, amenenso ali Mfumu yolamula mafumu onse a pa dziko lapansi. Iyeyo amatikonda, ndipo ndi magazi ake adatimasula ku machimo athu. Iye adatisandutsa mafumu, kuti tizitumikira Mulungu Atate ake modzipereka ngati mtundu wa ansembe. Motero Yesu Khristuyo alandire ulemerero ndi mphamvu zolamulira mpaka muyaya. Amen. Mvetsetsani! Akubwera pa mitambo! Aliyense adzamuwona, amene adamubaya aja nawonso adzamuwona. Ndipo anthu a mitundu yonse pansi pano adzalira chifukwa cha Iye. Nzoonadi zimenezi. Ndithudi! “Ine ndine Woyamba ndiponso Wotsiriza,” akutero Ambuye Mulungu, Mphambe, amene alipo, amene analipo kale, amene alikudza. Ndine, Yohane, mbale wanu, ndipo ngati mnzanu wokhulupirira Yesu, ndili nanu limodzi mu ufumu wa Mulungu, komanso m'masautso ndi m'kupirira kosatepatepa. Ndidaponyedwa pa chilumba cha Patimosi, chifukwa cha kulalika mau a Mulungu ndi kuchitira Yesu umboni. Pa tsiku la Ambuye ndidaagwidwa ndi Mzimu Woyera, nkumva kumbuyo kwanga liwu lamphamvu ngati kulira kwa lipenga. Liwulo lidati, “Zimene ukuwonazi, uzilembe m'buku ndipo ulitumize kwa mipingo isanu ndi iŵiri iyi: wa ku Efeso, wa ku Smirina, wa ku Pergamo, wa ku Tiatira, wa ku Sardi, wa ku Filadelfiya ndi wa ku Laodikea.” Nditacheuka kuti ndiwone akundilankhula ndani, ndidaona ndodo zoikapo nyale zisanu ndi ziŵiri zagolide. Pakati pake pa ndodo za nyalezo ndidaona wina wooneka ngati mwana wa munthu. Anali atavala mkanjo wautali, atamangira lamba wagolide pa chifuwa. Tsitsi lake linali loyera ngati thonje loyera kwambiri, ngati chipale chambee; maso ake ngati malaŵi a moto; mapazi ake ali chezichezi ngati mkuŵa woyeretsedwa m'ng'anjo ya moto; liwu lake ngati mkokomo wa madzi ochuluka. M'dzanja lake lamanja adaanyamula nyenyezi zisanu ndi ziŵiri, ndipo m'kamwa mwake munali lupanga lakuthwa konsekonse lotulukira kunja. Nkhope yake inali yoŵala ngati dzuŵa lamasana. Nditamuwona, ndidagwa kumapazi kwake ngati munthu wakufa. Koma Iye adandisanjika dzanja lake lamanja nati, “Usaope. Woyamba ndiponso Wotsiriza ndine. Wamoyo uja ndine. Ndidaafa, koma tsopano ndili moyo mpaka muyaya. Imfa ndi Malo a anthu akufa makiyi ake ali ndi Ine. Lemba tsono zimene waziwona, ndiye kuti zimene zikuchitika tsopano ndi zimene zidzachitike bwino lino. Chinsinsi cha nyenyezi zisanu ndi ziŵiri zija zimene waziwona m'dzanja langa lamanja, ndi china chija cha ndodo za nyale zisanu ndi ziŵiri zagolide, tanthauzo lake ndi ili: Nyenyezi zisanu ndi ziŵiri zija ndi atsogoleri a mipingo isanu ndi iŵiri; ndodo za nyale zisanu ndi ziŵiri zija ndi mipingo isanu ndi iŵiri imene.” “Mtsogoleri wa mpingo wa ku Efeso umlembere kuti, Naŵa mau ochokera kwa uja wanyamula nyenyezi zisanu ndi ziŵiri m'dzanja lake lamanja, ndi kuyenda pakati pa ndodo za nyale zisanu ndi ziŵiri zagolide zija. Akuti: Ntchito zanu zonse ndikuzidziŵa. Ndikudziŵa kuti mwakhala mukugwira ntchito kolimba, ndipo kuti muli ndi kupirira kosatepatepa. Ndikudziŵanso kuti anthu ochimwa simungaŵalekerere. Anthu amene amadzitcha atumwi, pamene sali atumwi konse, mwaŵayesa, ndipo mwaŵapeza kuti ngonama. Ndinudi opirira kolimba, ndipo mwasauka kwambiri chifukwa cha Ine, osatopa. Komatu pokudzudzulirani palipo: ndi apa pakuti mwasiya chikondi chimene munkandikonda nacho poyamba paja. Kumbukirani tsono kuti munali okwera kwambiri musanagwe; nchifukwa chake mutembenuke mtima, muzichitanso zija munkachita poyambazi. Mukapanda kutero, ndidzabwera nkudzachotsa ndodo ya nyale yanu pamalo pake. Komabe chokomera chanu ndi ichi chakuti, mumadana ndi zochita za Anikolai, zimene inenso ndimadana nazo. “Amene ali ndi makutu, amvetsetse zimene Mzimu Woyera akuuza mipingozi. “Amene adzapambane, ndidzampatsa mwai wodya zipatso za mtengo wopatsa moyo umene uli ku Paradizo la Mulungu Kumwamba.” “Mtsogoleri wa mpingo wa ku Smirina umlembere kuti: Naŵa mau ochokera kwa Iye amene ali Woyamba ndiponso Wotsiriza, amene adaafa nkukhalanso moyo. Akuti: Ndikudziŵa masautso anu ndiponso umphaŵi wanu, koma kwenikweni ndinu olemera. Ndikudziŵanso zomwe amakusinjirirani anthu amene amanama kuti ndi Ayuda, pamene sali Ayuda konse, koma ndi a mpingo wa Satana. Musachite nazo mantha zoŵaŵa zimene mukukakumana nazo. Ndithu enanu Satana adzakuponyetsani m'ndende kuti akuyeseni, ndipo mudzazunzika pa masiku khumi. Khalani okhulupirika mpaka kufa, ndipo ndidzakupatsani moyo ngati mphotho yanu. “Amene ali ndi makutu, amvetsetse zimene Mzimu Woyera akuuza mipingozi. “Amene adzapambane, siidzamkhudza imfa yachiŵiri.” “Mtsogoleri wa mpingo wa ku Pergamo umlembere kuti: Naŵa mau ochokera kwa uja ali ndi lupanga lakuthwa konsekonse lija. Akuti: Ndikudziŵako kumene inuyo mumakhala, ndiye kuti kumene kuli mpando wachifumu wa Satana. Inu ndinu okhulupirika kwa Ine, simudataye chikhulupiriro chanu, ngakhale pa nthaŵi ya Antipa, mboni yanga, munthu wanga wokhulupirika. Paja iye uja adamuphera kwanu komwe, kumene amakhala Satana. Koma pali zinthu zingapo zoti ndikudzudzulireni. Kwanuko muli ndi anthu ena otsata chiphunzitso cha Balamu mneneri wonama uja. Iye uja adaaphunzitsa mfumu Balaki kukopa Aisraele kuti azidya za nsembe zoperekedwa kwa mafano, ndi kumachita chigololo. Chimodzimodzi inuyo, muli nawonso anthu ena otsata chiphunzitso cha Anikolai. Mutembenuke mtima tsono. Mukapanda kutero, ndidzabwera kwanuko posachedwa, ndipo ndidzakuthirani nkhondo ndi lupanga lotulukira m'kamwa mwanga lija. “Amene ali ndi makutu, amvetsetse zimene Mzimu Woyera akuuza mipingozi. “Amene adzapambane, ndidzampatsako chakudya chobisika cha mana. Ndidzampatsanso mwala woyera wolembedwapo dzina latsopano, lodziŵa iye yekha, osati wina aliyense.” “Mtsogoleri wa mpingo wa ku Tiatira umlembere kuti: Naŵa mau ochokera kwa Mwana wa Mulungu, uja ali ndi maso onyezimira ngati malaŵi a moto, ndi mapazi onga chitsulo choŵala. Akuti: Ntchito zanu zonse ndikuzidziŵa. Ndikudziŵa chikondi chanu, kukhulupirika kwanu, kutumikira kwanu, ndi kupirira kwanu kosatepatepa. Ndikudziŵa kuti ntchito zanu zatsopano nzabwino koposa zoyamba zija. Komatu pokudzudzulirani palipo: ndi apa pakuti mumamlekerera mkazi uja Yezebele, amene amadzitcha mneneri. Iye uja amanyenga atumiki anga nkumaŵaphunzitsa kuti azichita dama ndi kumadya zansembe zoperekedwa kwa mafano. Ndidampatsa nthaŵi kuti atembenuke mtima, koma safuna kutembenuka ndi kuleka kusakhulupirika kwake. Tsono ndidzamgwetsa m'matenda, ndipo ochita naye dama lakelo, ndidzaŵagwetsa m'masautso aakulu, akapanda kutembenuka mtima ndi kuleka zoipa zonse zimene ankachita naye. Ana akenso ndidzaŵapha. Motero mipingo yonse idzazindikira kuti Ine ndine uja ndimadziŵa za m'mitima mwa anthu ndi za m'maganizo mwao. Aliyense mwa inu ndidzachita naye molingana ndi ntchito zake. “Koma enanu a ku Tiatira simudatsate nao chiphunzitso choipachi, ndipo simudaphunzireko zimene iwo amati zinsinsi zozama za Satana. Kwa inu mau anga ndi akuti sindikuwonjezerani malamulo ena, koma inu, mungogwiritsa zimene mudaphunzira, mpaka Ine ndidzabwere. Amene adzapambane ndi kuchita mpaka potsiriza zimene ndamlamula, ndidzampatsa ulamuliro pa mitundu yonse ya anthu. Adzailamulira ndi ndodo yachitsulo, nadzaiphwanyaphwanya ngati mbiya. Ulamuliro umenewu ndi womwe Ine ndidaulandira kwa Atate. Ndidzampatsanso Nthanda, nyenyezi yoŵala m'mamaŵa ija. “Amene ali ndi makutu, amvetsetse zimene Mzimu Woyera akuuza mipingozi.” “Mtsogoleri wa mpingo wa ku Sardi umlembere kuti, Naŵa mau ochokera kwa amene amalamulira mizimu ya Mulungu isanu ndi iŵiri ija, ndi nyenyezi zisanu ndi ziŵiri zija zili m'manja mwakezi. Akuti: Ntchito zanu zonse ndikuzidziŵa. Ndikudziŵa kuti muli ndi mbiri yoti ndinu amoyo, chonsecho ndinu akufa. Dzukani, ndi kulimbitsa zokutsalirani zimene zili pafupi kutha. Pakuti ndikuwona kuti ntchito zanu sizili zangwiro konse pamaso pa Mulungu wanga. Tsono kumbukirani zimene mudaphunzira, ndi zimene mudamva. Muzisunge ndipo mutembenuke mtima. Mukapanda kudzuka, ndidzabwera mwadzidzidzi ngati mbala, mwakuti nthaŵi imene ndidzakupezeniyo simudzaidziŵa. Koma alipo angapo pakati panu ku Sardi amene sadadetse zovala zao. Iwowo adzayenda nane pamodzi atavala zoyera, pakuti ndi oyeneradi. Motero aliyense amene adzapambane, adzamuvekanso zovala zoyera. Dzina lake sindidzalifafaniza m'buku la amoyo, ndipo ndidzamchitira umboni pamaso pa Atate anga, ndi pamaso pa angelo ao. “Amene ali ndi makutu, amvetsetse zimene Mzimu Woyera akuuza mipingozi.” “Mtsogoleri wa mpingo wa ku Filadelfiya umlembere kuti, Naŵa mau ochokera kwa Iye amene ali woyera ndi woona, amene ali ndi kiyi yaulamuliro ya Mfumu Davide. Uja amene amati akatsekula, palibe wotinso nkutseka, ndipo akatseka, palibe wotinso nkutsekula. Akuti: Ntchito zanu zonse ndikuzidziŵa. Ndakutsekulirani pa khomo, ndipo palibe amene angatsekepo. Ndikudziŵa kuti mphamvu zanu nzochepa, komabe mwasunga mau anga, ndipo simudandikane. Alipo ena a mpingo wa Satana, amene sali Ayuda, koma amanama kuti ndi Ayuda. Iwoŵa ndidzaŵabweretsa kwa inu kuti adzadzigwetse kumapazi kwanu. Pamenepo adzadziŵa kuti ndimakukondani. Popeza kuti mwasunga mau anga oti mupirire mosatepatepa, Inenso ndidzakusungani pa nthaŵi yamayeso imene ilikudza m'dziko lonse lapansi, kuti anthu onse okhalamo adzayesedwe. Ndikubwera posachedwa. Gwiritsani chimene muli nacho, kuti wina angakulandeni mphotho yanu. Amene adzapambane, ndidzamsandutsa mzati wokhazikika m'Nyumba ya Mulungu wanga. Sadzatulukamonso, ndipo pa iye ndidzalemba dzina la Mulungu wanga, ndi la mzinda wa Mulungu wanga. Mzindawo ndi Yerusalemu watsopano, wotsika Kumwamba kuchokera kwa Mulungu wanga. Pa iye ndidzalembanso dzina langa latsopano. “Amene ali ndi makutu, amvetsetse zimene Mzimu Woyera akuuza mipingozi.” “Mtsogoleri wa mpingo wa ku Laodikea umlembere kuti, Naŵa mau ochokera kwa Iye amene amatchedwa Amen uja, amene ali mboni yokhulupirika ndi yoona, ndiponso gwero la zolengedwa zonse za Mulungu. Akuti: Ntchito zanu zonse ndikuzidziŵa. Sindinu ozizira, sindinunso otentha. Bwenzi zili bwino mukadakhala ozizira kapena otentha. Koma popeza kuti ndinu ofunda chabe, osati otentha kapena ozizira, ndidzakusanzani. Paja inu mumati, ‘Ndife olemera, ndife achuma, sitisoŵa kanthu;’ osadziŵa kuti ndinu ovutika, ochititsa chifundo, amphaŵi, akhungu ndi amaliseche. Choncho ndikukulangizani kuti mugule kwa Ine golide woyeretsedwa ndi moto, kuti mukhale olemera. Mugulenso kwa Ine zovala zoyera, kuti muvale ndi kubisa maliseche anu ochititsa manyaziwo. Ndiponso mugule kwa Ine mankhwala a maso kuti mupenye. Onse amene ndimaŵakonda, ndimaŵadzudzula ndi kuŵalanga motero. Tsono chitani khama, mutembenuke mtima. Ndaima pakhomo pano, ndipo ndikugogoda. Wina akamva mau anga, nkutsekula chitseko, ndiloŵa, ndipo Ine ndi iye tidyera limodzi. Amene adzapambane, ndidzamlola kukhala nane pamodzi pa mpando wanga wachifumu, monga momwe ndidachitira Ineyo: ndidapambana, ndipo ndikukhala pamodzi ndi Atate anga pa mpando wao wachifumu. “Amene ali ndi makutu, amvetsetse zimene Mzimu Woyera akuuza mipingozi.” Pambuyo pake nditayang'ana, ndidaona pakhomo potsekuka Kumwamba. Ndipo ndidamva wina akulankhula nane ndi liwu lomwe ndidaamva poyamba lija, limene linkamveka ngati kulira kwa lipenga. Adandiwuza kuti, “Bwera Kumwamba kuno, ndidzakuwonetse zimene ziyenera kuchitika bwino lino.” Nthaŵi yomweyo ndidagwidwa ndi Mzimu Woyera. Kumwambako ndidaona mpando wachifumu, wina atakhalapo pampandopo. Amene adaakhala pampandoyo, maonekedwe ake anali oŵala ngati miyala yoyera ndi yofiira, yonyezimira. Pozungulira mpando wachifumuwo panali utawaleza, maonekedwe ake ngati mwala woŵala, wobiriŵira. Pozungulira mpando wachifumu pomwepo panali mipando inanso 24 yachifumu, ndipo pamipandopo padaakhala Akuluakulu 24, atavala zovala zoyera, ali ndi zisoti zachifumu zagolide pamutu. Mu mpando wachifumu munkatuluka mphezi, phokoso ndi mabingu. Patsogolo pake pa mpando womwewo pankayaka miyuni isanu ndi iŵiri, ndiye kuti mizimu ya Mulungu isanu ndi iŵiri. Patsogolo pake panalinso ngati nyanja yagalasi yonyezimira. Pakatimpakati, pozungulira mpando wachifumu uja, panali Zamoyo zinai, zokhala ndi maso ponseponse, kutsogolo ndi kumbuyo komwe. Chamoyo choyamba chinkaoneka ngati mkango, chachiŵiri ngati ng'ombe, chachitatu chinali ndi nkhope ya munthu, ndipo chachinai chinkaoneka ngati chiwombankhanga chouluka. Chamoyo chilichonse chinali ndi mapiko asanu ndi limodzi, ndipo zinali ndi maso ponseponse ndi m'kati momwe. Usana ndi usiku zimaimba mosalekeza kuti, “Ngoyera, ngoyera, ngoyera Ambuye, Mulungu Mphambe, amene analipo, amene alipo, amene alikudza.” Zamoyozo zimapereka ulemerero, ulemu ndi mayamiko kwa uja wokhala pa mpando wachifumuyu, amene ali ndi moyo wamuyaya. Pamene zikuchitika zimenezi, Akuluakulu 24 aja amadzigwetsa pamaso pa wokhala pa mpando wachifumuyo, ndi kumpembedza wokhala ndi moyo wamuyayayo. Ndipo amaponya pansi zisoti zao zaufumu patsogolo pa mpando wachifumuwo ndi kunena kuti, “Inu Ambuye athu ndi Mulungu wathu, ndinu oyenera kulandira ulemerero, ulemu ndi mphamvu, pakuti ndinu mudalenga zinthu zonse. Mudafuna kuti zonsezo zikhalepo, ndipo zidalengedwa.” Pambuyo pake ndidaona buku m'dzanja lamanja la wokhala pa mpando wachifumu uja. Bukulo linali lolembedwa m'kati ndi kumbuyo komwe, ndipo linali lomatidwa ndi zimatiro zisanu ndi ziŵiri. Kenaka ndidaona mngelo wamphamvu akufunsa mokweza mau kuti, “Ndani ali woyenera kufutukula bukuli ndi kumatula zimatiro zake?” Koma panalibe ndi mmodzi yemwe Kumwamba, kapena pa dziko lapansi, kapena kunsi kwa dziko, wotha kufutukula bukulo kapena kuyang'anamo. Motero ndidalira kwambiri poona kuti sadapezeke woyenera kufutukula bukulo kapena kuyang'anamo. Apo mmodzi mwa Akuluakulu aja adandiwuza kuti, “Usalire, pakuti Mkango wa m'fuko la Yuda, chidzukulu cha mfumu Davide, wapambana, ndipo Iye angathe kufutukula bukulo ndi kumatula zimatiro zake zisanu ndi ziŵiri zija.” Tsono ndidaona Mwanawankhosa ataimirira pakati pa mpando wachifumu uja ndi Zamoyo zinai zija ndiponso Akuluakulu 24 aja. Mwanawankhosayo ankaoneka ngati wophedwa, ndipo anali ndi nyanga zisanu ndi ziŵiri ndiponso maso asanu ndi aŵiri. Masowo ndi Mizimu isanu ndi iŵiri ija ya Mulungu yotumidwa m'dziko lonse lapansi. Iyeyo adabwera nkulandira buku lija limene linali m'dzanja lamanja la wokhala pampando wachifumu uja. Pamene adalilandira, Zamoyo zinai zija, pamodzi ndi Akuluakulu 24 aja, zidagwa pansi pamaso pa Mwanawankhosayo. Aliyense mwa Akuluakuluwo anali ndi zeze ndiponso mikhate yagolide yodzaza ndi lubani. Lubaniyo ndi mapemphero a anthu a Mulungu. Ankaimbira Mwanawankhosa uja nyimbo yatsopano iyi yakuti: “Ndinu oyenera kulandira bukuli ndi kumatula zimatiro zake. Pakuti mudaaphedwa, ndipo ndi imfa yanu mudaombolera Mulungu anthu a fuko lililonse, a chilankhulo chilichonse, ndi a mtundu uliwonse. Mudaŵasandutsa mtundu wachifumu ndi ansembe otumikira Mulungu wathu, ndipo adzakhala olamulira pa dziko lapansi.” Pambuyo pake nditayang'ana ndidaona namtindi wa angelo zikwizikwi pozungulira mpando wachifumu uja, Zamoyo zinai zija ndi Akuluakulu aja. Ndidamva angelowo akuimba mokweza mau kuti, “Mwanawankhosa amene adaaphedwayu, ngwoyenera kulandira mphamvu, chuma, nzeru, nyonga, ulemu, ulemerero ndi chiyamiko.” Ndidamvanso mau a cholengedwa chilichonse chakuthambo, cha pa dziko lapansi, cha kunsi kwa dziko, ndiponso cham'nyanja. Zolengedwa zonsezo zinkaimba mau akuti, “Wokhala pa mpando wachifumu uja, ndiponso Mwanawankhosa, alandire chiyamiko, ulemu, ulemerero ndi nyonga mpaka muyaya.” Apo Zamoyo zinai zija zidati, “Amen.” Ndipo Akuluakulu aja adadzigwetsa pansi moŵerama, napembedza. Pambuyo pake ndidaona Mwanawankhosa uja akumatula chimodzi mwa zimatiro zisanu ndi ziŵiri zija. Ndipo ndidamva chimodzi mwa Zamoyo zinai zija chikunena ndi liwu lomveka ngati bingu kuti, “Bwera!” Nditayang'ana, ndidaona kavalo woyera. Wokwerapo wake anali ndi uta, ndipo adaapatsidwa chisoti chaufumu. Adatulukira ngati wogonjetsa kuchokera kumwamba, kuti akagonjetsenso ena pa dziko lapansi. Kenaka Mwanawankhosa uja adamatula chimatiro chachiŵiri. Ndipo ndidamva Chamoyo chachiŵiri chija chikunena kuti, “Bwera!” Pamenepo kavalo wina, wofiira, adatulukira. Wokwerapo wake adaalandira mphamvu zothira nkhondo pa dziko lapansi, kuti anthu aziphana. Choncho adampatsa lupanga lalikulu. Pambuyo pake Mwanawankhosa uja adamatula chimatiro chachitatu. Ndipo ndidamva Chamoyo chachitatu chija chikunena kuti, “Bwera!” Nditayang'ana, ndidaona kavalo wakuda. Wokwerapo wake anali ndi sikelo m'manja. Tsono ndidamva ngati liwu kuchokera pakati pa Zamoyo zinai zija. Lidati, “Nsengwa imodzi ya tirigu, mtengo wake ndi malipiro a tsiku limodzi. Ndipo nsengwa zitatu za barele, mtengo wake ndi womwewonso. Koma usaononge mitengo ya mafuta ndi ya mphesa.” Kenaka Mwanawankhosa uja adamatula chimatiro chachinai. Ndipo ndidamva Chamoyo chachinai chija chikunena kuti, “Bwera!” Nditayang'ana, ndidaona kavalo wotuŵa. Wokwerapo wake dzina lake anali Imfa, ndipo Malo a anthu akufa ankamutsata pambuyo. Aŵiriwo adaalandira ulamuliro pa chimodzi mwa zigawo zinai za dziko lapansi, kuti aphe anthu ndi nkhondo, njala, nthenda, ndi zilombo zolusa. Zitatha izi, Mwanawankhosa uja adamatula chimatiro chachisanu. Ndipo ndidaona kunsi kwa guwa lansembe mizimu ya anthu amene adaphedwa chifukwa cha kulalika mau a Mulungu, ndiponso chifukwa chochitira mauwo umboni wamphamvu. Mizimuyo idafuula mokweza mau kuti, “Ambuye, Inu ndinu Mfumu yathu yoyera ndi yoona. Mudzaŵalekerera mpaka liti osaŵaimba mlandu ndi kuŵalanga anthu aja okhala pansi pano amene adatipha?” Apo aliyense adapatsidwa mkanjo woyera, ndipo adamva mau akuti, “Bapumulani pang'ono mpaka chitakwanira chiŵerengero chathunthu cha atumiki anzanu ndi abale anu, amene nawonso ayenera kuphedwa monga inu nomwe.” Pambuyo pake Mwanawankhosa uja adamatula chimatiro chachisanu ndi chimodzi. Ndipo padachitika chivomezi champhamvu. Dzuŵa lidadzangoti bii ngati chiguduli chakuda, mwezi wathunthu nkungoti psuu ngati magazi. Nyenyezi zakuthambo zidagwa pansi, ngati muja zimayoyokera nkhuyu zaziŵisi, mkuyu ukamagwedezeka ndi mphepo yamkuntho. Thambo lidachoka monga momwe imakulungidwira mphasa akamaiyalula. Ndipo phiri lililonse ndi chilumba chilichonse zidachotsedwa m'malo mwake. Apo mafumu a dziko lapansi, atsogoleri a dziko, akulu a ankhondo, anthu olemera, anthu amphamvu, akapolo onse ndi mfulu zonse, onsewo adakabisala m'mapanga ndi m'matanthwe am'mapiri. Iwowo ankafuulira mapiri ndi matanthwewo kuti, “Tigwereni ndi kutivundikira, kuti wokhala pa mpando wachifumu uja angatiwone, ndipo kuti tipulumuke ku chilango cha Mwanawankhosayo. Lafikadi tsiku loopsa la mkwiyo wao, ndipo angathe kulimbapo ndani?” Pambuyo pake ndidaona angelo anai ataimirira pa mbali zinai za dziko lapansi. Anali atagwira mphepo zinai za dziko lapansi kuti ndi imodzi yomwe isaombe pa dziko, kapena pa nyanja, kapena pa mtengo uliwonse. Kenaka ndidaona mngelo wina akukwera kuchokera kuvuma, ali ndi chidindo cha Mulungu wopatsa moyo. Mokweza mau adafuulira angelo anai aja amene Mulungu adaaŵapatsa mphamvu yoonongera dziko ndi nyanja. Adaŵauza kuti, “Musaononge msanga dziko, kapena nyanja, kapenanso mitengo, tiyambe taŵalemba chizindikiro pa mphumi atumiki a Mulungu wathu.” Tsono ndidamva chiŵerengero cha olembedwa chizindikiro aja. Chidakwanira zikwi 144, ndipo olembedwa chizindikirowo anali a m'fuko lililonse la Aisraele. Olembedwa chizindikiro: A m'fuko la Yuda anali zikwi khumi ndi ziŵiri. A m'fuko la Rubeni anali zikwi khumi ndi ziŵiri. A m'fuko la Gadi anali zikwi khumi ndi ziŵiri. A m'fuko la Asere anali zikwi khumi ndi ziŵiri. A m'fuko la Nafutali anali zikwi khumi ndi ziŵiri. A m'fuko la Manase anali zikwi khumi ndi ziŵiri. A m'fuko la Simeoni anali zikwi khumi ndi ziŵiri. A m'fuko la Levi anali zikwi khumi ndi ziŵiri. A m'fuko la Isakara anali zikwi khumi ndi ziŵiri. A m'fuko la Zebuloni anali zikwi khumi ndi ziŵiri. A m'fuko la Yosefe anali zikwi khumi ndi ziŵiri. A m'fuko la Benjamini anali zikwi khumi ndi ziŵiri. Pambuyo pake nditayang'ana, ndidaona chinamtindi cha anthu osaŵerengeka. Anthuwo anali ochokera m'mitundu yonse ya anthu, ndi m'mafuko onse, ndipo anali a zilankhulo zonse. Adaimirira patsogolo pa mpando wachifumu uja ndi pamaso pa Mwanawankhosa uja; anali atavala mikanjo yoyera, nthambi zakanjedza zili m'manja. Ankafuula mokweza mau kuti, “Chipulumutso nchochokera kwa Mulungu wathu wokhala pa mpando wachifumu, ndiponso kwa Mwanawankhosa.” Angelo onse adaimirira kuzungulira mpando wachifumu uja, kuzunguliranso Akuluakulu aja ndi Zamoyo zinai zija. Angelowo adadzigwetsa chafufumimba patsogolo pa mpando wachifumuwo, napembedza Mulungu. Adati, “Amen! Mulungu wathu alandire matamando, ulemerero, nzeru, chiyamiko, ulemu, mphamvu ndi nyonga mpaka muyaya. Amen.” Pamenepo mmodzi mwa Akuluakulu aja adandifunsa kuti, “Kodi ovala mikanjo yoyeraŵa ndani, ndipo achokera kuti?” Ine ndidati, “Mbuyanga, mukudziŵa ndinu.” Ndipo iye adandiwuza kuti, “Ameneŵa ndi amene adapambana m'masautso aakulu aja. Adachapa mikanjo yao ndi kuiyeretsa m'magazi a Mwanawankhosa. “Nchifukwa chake ali pamaso pa mpando wachifumu wa Mulungu, ndipo amampembedza m'Nyumba mwake usana ndi usiku. Wokhala pa mpando wachifumu uja adzakhala ngati hema lao loŵateteza. Iwo sadzamvanso njala kapena ludzu. Sadzaombedwanso ndi dzuŵa kapena kusauka ndi kutentha. Pakuti Mwanawankhosa uja amene ali pakatikati pa mpando wachifumu, adzakhala Mbusa wao, adzaŵatsogolera ku akasupe a madzi amoyo. Ndipo Mulungu adzaŵapukuta misozi yonse m'maso.” Pomaliza Mwanawankhosa uja adamatula chimatiro chachisanu ndi chiŵiri. Pamenepo onse Kumwamba adangoti chete pa hafu la ora. Kenaka ndidaona angelo asanu ndi aŵiri aja amene amaimirira pamaso pa Mulungu, akupatsidwa malipenga asanu ndi aŵiri. Mngelo wina adabwera naimirira ku guwa lansembe ali ndi chofukizira chagolide. Adapatsidwa lubani wambiri kuti ampereke pamodzi ndi mapemphero a anthu a Mulungu pa guwa lagolide patsogolo pa mpando wachifumu uja. Pamodzi ndi mapemphero a anthu a Mulunguwo, utsi wa lubaniyo udakwera pamaso pa Mulungu kuchokera m'manja mwa mngelo uja. Pamenepo mngeloyo adatenga chofukiziracho nachidzaza ndi moto wochokera ku guwa lija. Adachiponya pa dziko lapansi, ndipo nthaŵi yomweyo padachitika mabingu, phokoso, mphezi ndi chivomezi. Tsono angelo asanu ndi aŵiri amene anali ndi malipenga asanu ndi aŵiri aja adakonzeka kuti alize malipengawo. Mngelo woyamba adaliza lipenga lake. Atatero, padadza matalala ndi moto zosanganizika ndi magazi. Zimenezi zidaponyedwa pa dziko lapansi, ndipo chimodzi mwa zigawo zitatu za dziko ndi za mitengo chidapsa. Pamenepo padapsanso udzu wonse wauŵisi. Mngelo wachiŵiri adaliza lipenga lake. Atatero, chinthu chooneka ngati chiphiri choyaka moto chidaponyedwa m'nyanja. Pomwepo chimodzi mwa zigawo zitatu za nyanja chidasanduka magazi, ndipo chimodzi mwa zigawo zitatu za zolengedwa zonse zamoyo zam'nyanjamo chidafa. Chimodzinso mwa zigawo zitatu za zombo chidaonongeka. Mngelo wachitatu adaliza lipenga lake. Atatero chinyenyezi choyaka ngati muuni chidagwa kuchokera kuthambo. Chidagwera pa chimodzi mwa zigawo zitatu za mitsinje, ndi pa akasupe. Chinyenyezicho dzina lake ndi “Kuŵaŵa”. Chimodzi mwa zigawo zitatu za madzi chidasanduka choŵaŵa, mwakuti anthu ambiri adafa nawo madziwo chifukwa cha kuŵaŵa kwakeko. Mngelo wachinai adaliza lipenga lake. Atatero chimodzichimodzi mwa zigawo zitatuzitatu za dzuŵa, za mwezi ndi za nyenyezi chidamenyedwa. Zitachitika zimenezi, chimodzi mwa zigawo zitatu za zonsezo chidada. Panalibenso kuŵala pa chimodzi mwa zigawo zitatu za usana, ndi chimodzimodzinso usiku. Pambuyo pake ndidayang'ana, ndipo ndidaona chiwombankhanga chikuuluka mu mlengalenga, ndipo ndidamva chikulira mokweza kuti, “Tsoka! Tsoka! Tsoka kwa anthu onse okhala pa dziko lapansi, angelo atatu otsala aja akangoliza malipenga ao.” Pamenepo mngelo wachisanu adaliza lipenga lake. Atatero ndidaona nyenyezi itagwa pansi kuchokera ku thambo. Idapatsidwa kiyi ya dzenje lopita ku Chiphompho chakuya. Nyenyeziyo idatsekula padzenjepo, ndipo padatuluka utsi wonga wam'ching'anjo. Dzuŵa ndi thambo zidada chifukwa cha utsi wotuluka m'dzenjewo. Muutsimo mudatuluka dzombe kukaloŵa m'dziko lapansi, ndipo dzombelo lidapatsidwa mphamvu zoluma zonga za zinkhanira za pa dziko lapansi. Dzombelo lidalamulidwa kuti lisaononge udzu wa pa dziko lapansi, kapena chomera chilichonse, kapena mtengo uliwonse. Lidaloledwa kungoononga anthu opanda chizindikiro cha Mulungu chija pamphumi pao. Silidaloledwe kuŵapha, koma kungoŵazunza pa miyezi isanu. Kuŵaŵa kwake kwa mazunzowo kunkalingana ndi ululu wa chinkhanira chikaluma munthu. Masiku amenewo anthuwo adzafunafuna imfa, koma osaipeza. Adzafunitsitsa kufa, koma imfa izidzaŵathaŵa. Dzombelo linkaoneka ngati akavalo okonzekera nkhondo. Pamitu pake panali ngati zisoti zaufumu zagolide, nkhope zake ngati za anthu. Tsitsi lake linali litalilitali ngati la azimai, mano ake ngati a mkango. Pachifuwa pake panali mamba onga ngati malaya achitsulo apachifuwa. Kulira kwa mapiko ake kunali ngati kwa magareta ankhondo ambiri okokedwa ndi akavalo othamangira ku nkhondo. Dzombelo lili ndi michira ngati zinkhanira, ndipo lili ndi mbola. Mphamvu yake ija yopwetekera anthu pa miyezi isanu inali kumichira kwake. Mfumu yake inali mngelo wolamulira Chiphompho chija. Pa Chiyuda dzina lake ndi Abadoni, pa Chigriki ndi Apoliyoni (tanthauzo lake ndiye kuti, “Woononga uja”.) Tsoka loyamba lija lapita. Atsalabe masoka enanso aŵiri oyenera kubwera. Mngelo wachisanu ndi chimodzi adaliza lipenga lake. Atatero ndidamva liwu lochokera ku ngodya zinai za guwa lagolide lija lokhala pamaso pa Mulungu. Liwulo lidauza mngelo wachisanu ndi chimodzi wokhala ndi lipenga uja, kunena kuti, “Amasule angelo anai aja amene ali omangidwa pa mtsinje waukulu wa Yufurate.” Adaŵamasuladi angelowo kuti akaphe chimodzi mwa zigawo zitatu za anthu onse. Angelowo Mulungu anali ataŵakonzera ora lake, tsiku lake, mwezi wake ndi chaka chake. Ndidamva chiŵerengero cha ankhondo a pa akavalo aja, kuti chinali mamiliyoni 200. M'masomphenya momwemo, akavalowo ndidaŵaona motere: okwerapo ake adaavala malaya achitsulo apachifuwa a maonekedwe ofiira ngati moto, obiriŵira ngati utsi, ndi achikasu ngati miyala ya sulufure. Mitu ya akavalowo inali ngati ya mikango, ndipo m'kamwa mwao munkatuluka moto, utsi ndi sulufure. Chimodzi mwa zigawo zitatu za anthu onse chidaphedwa ndi miliri itatu iyi: wa moto, wa utsi ndi wa sulufure, zimene zinkatuluka m'kamwa mwa akavalo aja. Akavalowo mphamvu zao zinali m'kamwa ndi ku michira. Michira yaoyo inali ngati njoka, yokhala ndi mitu yopwetekera anthu. Anthu ena onse otsala, amene sadaphedwe ndi miliri ija, sadatembenuke mtima kuti asiye ntchito za manja ao. Sadaleke kupembedza mizimu yoipa, ndi mafano agolide, asiliva, amkuŵa, ndi amtengo, amene sangathe kupenya, kapena kumva, kapena kuyenda. Anthuwo sadatembenukenso kuti aleke kupha anzao, ufiti, dama ndi kuba. Pambuyo pake ndidaona mngelo wina wamphamvu akutsika kuchokera Kumwamba. Adaavala mtambo, ndipo pozungulira mutu wake panali utawaleza. Nkhope yake inali ngati dzuŵa, miyendo yake ngati mizati yamoto. M'manja mwake anali ndi kampukutu kofutukula. Ndi mwendo wa ku dzanja lamanja adaaponda pa nyanja, ndi wakumanzere adaaponda pa mtunda. Tsono adaafuula mokweza ngati kubangula kwa mkango. Mngeloyo atangofuula choncho, mabingu asanu ndi aŵiri aja adagunda. Mabinguwo atangogunda, ndidaati ndilembe. Koma ndidamva mau ochokera Kumwamba akuti, “Zisunge mu mtima zimene mabingu asanu ndi aŵiri aja anena. Usazilembe.” Pamenepo mngelo amene ndidaaona ataponda pa nyanja ndi pa mtunda uja, adakweza dzanja lake lamanja kumwamba. Atatero adalumbira m'dzina la Mulungu wokhala ndi moyo mpaka muyaya, amene adalenga thambo lakumwamba ndi zonse zokhala kumeneko, dziko lapansi ndi zonse zokhala m'menemo, ndiponso nyanja ndi zonse zokhala m'menemo. Mngeloyo kulumbira kwake adati, “Pasakhalenso zochedwa tsopano. Pamene mngelo wachisanu ndi chiŵiri adzaliza lipenga lake, zachinsinsi zimene Mulungu adakonzeratu zidzachitika, monga momwe Iye adaalonjezera kwa atumiki ake aja, aneneri.” Pamenepo mau amene ndidaamva kuchokera Kumwamba adandilankhulanso, adati, “Pita, katenge kampukutu kofutukula kaja kamene kali m'manja mwa mngelo woponda pa nyanja ndi pa mtunda uja.” Ndidapitadi kwa mngeloyo nkumupempha kuti andipatse kampukutuko. Iye adati, “Kwaya, idya. M'mimba mwako kaziŵaŵa, koma m'kamwa mwako kazizuna ngati uchi.” Ndidalandira kampukutuko m'manja mwa mngelo uja, ndipo ndidadyadi. M'kamwamu kankazuna ngati uchi, koma nditakameza, m'mimbamu munkaŵaŵa. Pamenepo adandiwuza kuti, “Uyenera kulengezanso za mitundu yambiri ya anthu, za zilankhulo zosiyanasiyana, ndi za mafumu ambiri.” Pambuyo pake adandipatsa bango loyesera, longa ndodo, nandiwuza kuti, “Nyamuka, kayese Nyumba ya Mulungu ndi guwa lansembe, ndipo ukaŵerenge opembedza m'Nyumbamo. Koma bwalo la kunja kwa Nyumbayo ulisiye, osaliyesa. Bwalo limeneli lidapatsidwa kwa anthu akunja, ndipo iwowo adzaupondereza Mzinda woyerawo pa miyezi 42. Ndidzatuma mboni zanga ziŵiri zovala chiguduli, kuwonetsa chisoni, kuti zidzalalike mau ochokera kwa Mulungu pa masiku 1,260.” Mboni ziŵirizo ndi mitengo iŵiri ija ya olivi, ndi ndodo za nyale ziŵiri zija zimene zili pamaso pa Ambuye olamulira dziko lonse lapansi. Wina aliyense akafuna kuzipweteka mbonizo, moto umatuluka kukamwa kwao nkuwononga adani aowo. Ndipo munthu aliyense wofuna kuzipweteka, adzayenera kuphedwa mwa njira yomweyo. Mbonizo zili ndi mphamvu zomanga mvula kuti isagwe masiku amene iwo akulalika mau ochokera kwa Mulungu. Zili ndi mphamvu zosandutsira madzi kuti akhale magazi. Ndipo zili ndi mphamvu zodzetsera mliri uliwonse pa dziko lapansi, nthaŵi iliyonse imene zingafune. Tsono mbonizo zikadzatsiriza umboni waowo, chilombo chotuluka m'Chiphompho chija chidzachita nazo nkhondo. Chidzazigonjetsa nkuzipha. Mitembo yao idzakhala ili thasa pa mseu wa mu mzinda waukulu, kumene Ambuye ao adapachikidwa pa mtanda. Mokuluŵika mzindawo umatchedwa “Sodomu” mwina “Ejipito”. Anthu a mitundu yonse, a mafuko onse ndiponso a zilankhulo zonse azidzayang'anitsitsa mitemboyo masiku atatu ndi hafu, akukana kuti iikidwe m'manda. Ndipo anthu onse okhala pa dziko lapansi adzakondwera nazo zimenezi. Adzachita chikondwerero ndi kutumizirana mphatso, chifukwa aneneri aŵiriŵa ankaŵasautsa kwambiri anthu okhala pa dziko lapansiwo. Koma atatha masiku atatu ndi hafu aja, mpweya wopatsa moyo, wochokera kwa Mulungu, udaloŵa mwa aneneriwo. Motero adaimirira, ndipo onse amene adaŵaona adagwidwa ndi mantha aakulu. Aneneri aja adamva mau amphamvu ochokera Kumwamba oŵauza kuti, “Bwerani kuno.” Iwowo adapitadi Kumwamba mu mtambo, adani ao aja akuŵapenya. Nthaŵi yomweyo kudachita chivomezi chachikulu, mwakuti chimodzi mwa zigawo khumi za mzinda chidagwa, ndipo anthu zikwi zisanu ndi ziŵiri adaphedwa ndi chivomezicho. Otsalawo adaopsedwa kwambiri nayamba kutamanda Mulungu wa Kumwamba. Tsoka lachiŵiri lija lapita tsopano, koma lachitatu likubwera posachedwa. Pambuyo pake mngelo wachisanu ndi chiŵiri adaliza lipenga lake. Atatero kumwamba kudamveka mau okweza. Mauwo adati, “Tsopano mphamvu zolamulira dziko lapansi zili m'manja mwa Ambuye athu ndi mwa Wodzozedwa wake uja, ndipo adzalamulira mpaka muyaya.” Pamenepo Akuluakulu 24 aja okhala pa mipando yao yachifumu pamaso pa Mulungu, adadzigwetsa chafufumimba napembedza Mulungu. Adati, “Ambuye Mulungu, Mphambe, Inu amene mulipo ndipo munaliponso kale, tikukuyamikani chifukwa mwaonetsa mphamvu yanu yaikulu, ndipo mwayamba kukhazikitsa ufumu wanu. Anthu akunja adakalipa, koma yafika nthaŵi yoonetsa mkwiyo wanu, ndiye kuti nthaŵi yoweruza anthu akufa. Yafika nthaŵi yoti mupereke mphotho kwa atumiki anu, aneneri, ndi kwa anthu anu, ndiye kuti onse, ang'onoang'ono ndi akuluakulu, amene amaopa dzina lanu. Yafika nthaŵi yoti muŵaononge amene akuwononga dziko lapansi.” Pamenepo mudatsekuka m'Nyumba ya Mulungu Kumwamba, ndipo bokosi lachipangano lidaoneka m'Nyumbamo. Kenaka kudachita mphezi, phokoso, mabingu ndi chivomezi, ndipo kudagwa matalala akuluakulu. Pambuyo pake kudaoneka chizindikiro chachikulu kuthambo: mai atavala dzuŵa, mapazi ake ataponda pa mwezi, pamutu pake pali chisoti chaufumu cha nyenyezi khumi ndi ziŵiri. Maiyo anali ndi pathupi, ndipo pa nthaŵi yochira adalira nako mokuwa kupweteka kwa kubala. Kudaonekanso chizindikiro china kuthambo: chinjoka chachikulu, chofiira, cha mitu isanu ndi iŵiri ndi nyanga khumi; pa mutu uliwonse chitavala chisoti chaufumu. Ndi mchira wake chidakokolola chimodzi mwa zigawo zitatu za nyenyezi zakuthambo, nkuzigwetsa pa dziko lapansi. Chinjokacho chidadzaimirira pamaso pa mai uja amene anali pafupi kubala mwana, kuti akangobadwa mwanayo, chimudye. Maiyo adabala mwana wamwamuna, woyenera kudzalamulira anthu a mitundu yonse ndi ndodo yachitsulo. Mwanayo adalandidwa kumanja kwa mai wake kupita naye kwa Mulungu ndi ku mpando wake wachifumu. Apo mai uja adathaŵira ku chipululu. Kumeneko Mulungu adaakonzeratu malo ake, kuti akasamalidweko masiku 1,260. Tsono kudabuka nkhondo Kumwamba, Mikaele ndi angelo ake kumenyana ndi chinjoka chija. Chinjokacho pamodzi ndi angelo ake chidatengana nawo, koma onsewo adagonjetsedwa, mwakuti adataya malo ao Kumwamba. Chinjoka chachikulu chija chidagwetsedwa pansi. Ichocho ndiye njoka yakale ija yotchedwa “Mdyerekezi” ndiponso “Satana”, wonyenga anthu a pa dziko lonse lapansi. Chidagwetsedwa pa dziko lapansi pamodzi ndi angelo ake onse. Pamenepo ndidamva mau amphamvu Kumwamba akunena kuti, “Tsopano Mulungu wathu watipulumutsa. Waonetsa mphamvu zake ndi ufumu wake. Tsopano Wodzozedwa uja waonetsa ulamuliro wake. Woneneza abale athu uja wagwetsedwa pansi, amangokhalira kuŵaneneza kwa Mulungu wathu usana ndi usiku. Abale athuwo adamgonjetsa ndi magazi a Mwanawankhosa uja, ndiponso ndi mau amene iwo ankaŵachitira umboni. Iwo adadzipereka kotheratu, kotero kuti sadaope ngakhale kufa. Choncho kondwerani inu, Dziko la Kumwamba, ndi onse okhalamo. Koma muli ndi tsoka, inu dziko lapansi ndi nyanja, pakuti Satana adatsikira kwa inu, ali wokalipa kwambiri, chifukwa wadziŵa kuti yangomutsalira nthaŵi pang'ono.” Tsono chinjoka chija chitaona kuti chagwetsedwa pa dziko lapansi, chidayamba kumpirikitsa mai uja amene anali atabala mwana wamwamuna. Koma maiyo adapatsidwa mapiko aŵiri a chiwombankhanga chachikulu kuti athaŵire ku malo ake aja akuchipululu. Kumeneko adzasamalidwa zaka zitatu ndi hafu, kuwopa kuti chinjoka chija chingamuwone. Pamenepo chinjokacho chidalavulira mai uja madzi ochuluka ngati mtsinje, kuti amkokolole. Koma dziko lapansi lidamthandiza maiyo: lidayasama nkuumeza mtsinje umene chinjoka chija chidaalavula. Apo chinjokacho chidamupsera mtima kwambiri mai uja, nkungochokapo kuti chikayambane ndi ana ena onse a maiyo, ndiye kuti anthu otsata malamulo a Mulungu ndi kuchitira Yesu umboni. Motero chidakaimirira pambali pa nyanja. Pambuyo pake ndidaona chilombo chikuvuuka m'nyanja. Chinali ndi nyanga khumi ndi mitu isanu ndi iŵiri. Pa nyanga iliyonse chidaavala chisoti chaufumu, ndipo pa mutu uliwonse panali dzina lonyoza Mulungu. Chilombo chimene ndidaaonacho chinali ngati kambuku, mapazi ake ngati a chimbalangondo, kukamwa kwake ngati kwa mkango. Chinjoka chija chidaapatsa chilombocho mphamvu zake, mpando wake wachifumu, ndiponso ulamuliro waukulu. Umodzi mwa mitu yake unkaoneka ngati uli ndi bala lofa nalo, koma balalo linali litapola. Pamenepo anthu onse ankachitsata chilombocho ali odabwa. Adachipembedza chinjoka chija chifukwa chidaapatsa ulamuliro wake kwa chilombo chija. Nachonso chilombo chija adachipembedza nkumanena kuti, “Ndani angafanane ndi chilombochi? Ndani angachite nacho nkhondo?” Chilombo chija chidaloledwa kulankhula mau onyada ndi onyoza Mulungu mwachipongwe. Ndipo chidapatsidwa mphamvu zolamulira pa miyezi 42. Tsono chidayamba kunena mau achipongwe onyoza Mulungu, dzina lake, malo ake okhalamo, ndi onse okhala Kumwamba. Chidaloledwa kuŵathira nkhondo anthu a Mulungu ndi kuŵagonjetsa. Chidapatsidwanso mphamvu zolamulira anthu a fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi a chilankhulo chilichonse. Onse okhala pa dziko lapansi adzachipembedza, ndiye kuti aliyense amene, chilengedwere dziko lapansi, dzina lake silidalembedwe m'buku la amoyo la Mwanawankhosa adaphedwa uja. Ngati wina ali ndi makutu, amve. Woyenera kutengedwa ku ukapolo, kuukapoloko akapitadi. Woyenera kuphedwa ku nkhondo, kunkhondoko akaphedwadi. Pamenepa ndiye pamene anthu a Mulungu ayenera kuwonetsa kupirira ndi kulimbika m'chikhulupiriro. Kenaka ndidaona chilombo china chikutuluka pansi. Chinali ndi nyanga ziŵiri ngati mwanawankhosa, kulankhula kwake ngati kwa chinjoka. Chinkalamulira pamaso pa chilombo choyamba chija ndi mphamvu zimene chilombo choyambacho chidaachipatsa. Chinkakakamiza dziko lapansi ndi onse okhalamo kuti azipembedza chilombo choyamba chija chimene bala lake lofa nalo lija linali litapola. Chilombo chachiŵirichi chinkachita zozizwitsa kwambiri, mpaka kumadzetsa moto pa dziko lapansi kuchokera kumwamba, anthu akuwona. Chinkanyenganso anthu okhala pa dziko lapansi ndi zozizwitsa zimene chidaaloledwa kuchita pamaso pa chilombo choyamba chija. Chinkauza anthu okhala pa dziko lapansiwo kuti apange fano lolemekezera chilombo chimene chidaavulazidwa ndi lupanga, koma nkukhalabe moyo. Chidaaloledwa kuuzira mpweya wopatsa moyo mu fano la chilombo choyamba chija, kuti mpaka lizilankhula, ndi kuphetsa aliyense wosalipembedza. Chinkakakamiza anthu onse, ang'onoang'ono ndi akuluakulu, olemera ndi osauka, mfulu ndi akapolo, kuti alembedwe chizindikiro pa dzanja lamanja kapena pa mphumi. Chinkachita zimenezi kuti wina aliyense asaloledwe kugula kapena kugulitsa kanthu ngati alibe chizindikiro chimenechi, ndiye kuti dzina la chilombo choyamba chija, kapena nambala yotanthauza dzina lake. Pano pafunika nzeru. Yemwe ali ndi nzeru atanthauze nambala ya chilomboyo, pakuti nambalayo ikutanthauza munthu. Nambala yake ndi 666. Pambuyo pake nditayang'ana, ndidaona Mwanawankhosa ataimirira pa Phiri la Ziyoni. Pamodzi ndi Iye panali anthu zikwi 144, olembedwa dzina lake ndiponso dzina la Atate ake pamphumi pao. Tsono ndidamva liwu lochokera kumwamba longa ngati mkokomo wa madzi ambiri, ndiponso ngati kugunda kwamphamvu kwa bingu. Liwu limene ndidaamvalo linkamveka ngati anthu akuimba azeze ao. Anthu aja ankaimba nyimbo yatsopano pamaso pa mpando wachifumu uja ndi pamaso pa Zamoyo zinai zija, ndi Akuluakulu aja. Panalibe ndi mmodzi yemwe wotha kuiphunzira nyimboyo, kupatula anthu zikwi 144 aja amene anali ataomboledwa mu ukapolo wa dziko lapansi. Ndi ameneŵa amene ankadzisunga angwiro osadziipitsa ndi akazi. Ndi ameneŵa amene amatsata Mwanawankhosa uja kulikonse kumene akupita. Ndiwo amene adaomboledwa pakati pa anthu ena onse, kuti akhale oyambirira kuperekedwa kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa uja. Sadanenepo bodza konse. Alibe cholakwa. Pambuyo pake ndidaona mngelo wina akuuluka mu mlengalenga. Anali ndi Uthenga Wabwino wamuyaya woti akalalike kwa anthu okhala pa dziko lapansi, kwa anthu a mtundu uliwonse, a fuko lililonse, ndi a chilankhulo chilichonse. Mngeloyo adanena mokweza mau kuti, “Opani Mulungu ndi kumtamanda, pakuti yafika nthaŵi yoti aweruze anthu. Mumpembedze Iye amene adalenga thambo, dziko lapansi, nyanja, ndi akasupe a madzi.” Padafika mngelo wina wachiŵiri wotsatana ndi woyamba uja. Adati, “Wagwa, wagwa Babiloni wotchuka uja, amene ankamwetsa anthu a mitundu yonse vinyo wa zilakolako zake zadama.” Kenaka padafikanso mngelo wina wachitatu, wotsatana ndi aŵiri ena aja. Mokweza mau adati, “Aliyense wopembedza chilombo chija ndi fano lake, ndi kulembedwa chizindikiro pa mphumi kapena pa dzanja, nayenso adzamwako vinyo wa ukali wa Mulungu. Vinyo wake adzathiridwa, popanda kanthu kochepetsa mphamvu yake, m'chikho cha mkwiyo wa Mulungu. Munthuyo adzazunzidwa ndi moto ndi miyala yasulufure yoyaka. Zimenezi zidzachitikira pamaso pa angelo a Mulungu, ndi Mwanawankhosa uja. Utsi wa moto woŵazunzawo umakwera kumwamba mpaka muyaya. Anthu amene adapembedza chilombo chija ndi fano lake, ndiponso amene adalembedwa chizindikiro cha dzina lake chija, sapeza mpumulo usana kapena usiku. “Pamenepa mpofunika kuti anthu a Mulungu akhale opirira, amene amatsata malamulo ake ndipo ali ndi chikhulupiriro mwa Yesu.” Pambuyo pake ndidamva mau ochokera Kumwamba. Adati, “Lemba kuti, Ngodala anthu akufa amene kuyambira tsopano mpaka m'tsogolo muno afa ali otumikira Ambuye.” Mzimu Woyera akuti, “Inde, ngodaladi. Akapumule ntchito zao zolemetsa, pakuti ntchito zaozo zimaŵatsata.” Pambuyo pake nditayang'ana ndidaona mtambo woyera. Pamtambopo padaakhala wina ngati Mwana wa Munthu, kumutu atavala chisoti chaufumu chagolide, m'manjamu ali ndi chikwakwa chakuthwa. Mngelo wina adatuluka m'Nyumba ya Mulungu nafuula ndi mau amphamvu kwa Uja wokhala pamtamboyu. Adati, “Gwiritsa ntchito chikwakwa chako, yambapo kudula dzinthu. Tsopano nyengo yamasika yafika, ndipo dzinthu dza pa dziko lapansi dzidacha kale.” Pamenepo wokhala pamtambo uja adakayambadi ntchitoyo ndi chikwakwa chake, nadula dzinthu dzonse dza pa dziko lapansi. Pambuyo pake mngelo wina adatuluka m'Nyumba ya Mulungu Kumwamba. Nayenso anali ndi chikwakwa chakuthwa. Kenaka mngelo winanso, amene amalamulira moto, adatulukira kuchokera ku guwa lansembe. Adafuula ndi mau amphamvu kwa Uja wokhala ndi chikwakwa chakuthwa. Adati, “Gwiritsa ntchito chikwakwa chakocho, yambapo kudula mphesa za m'munda wamphesa wa pa dziko lapansi, pakuti mphesazo zidapsa kale.” Pamenepo mngelo uja adakayambadi ntchitoyo ndi chikwakwa chake, nadula mphesa zonse za pa dziko lapansi, nkuziponya m'chopondera mphesa cha ukali woopsa wa Mulungu. Mphesazo zidapondedwa m'chopondera mphesa kunja kwa mzinda. Ndipo m'chopondera mphesacho mudatuluka magazi nkumayenderera ngati mtsinje, kutalika kwake makilomita 300, kuzama kwake ngati mita ndi hafu. Pambuyo pake ndidaona Kumwamba chizindikiro china chachikulu ndi chododometsa: angelo asanu ndi aŵiri okhala ndi miliri isanu ndi iŵiri. Miliriyo ndi yotsiriza, pakuti ukali wa Mulungu uthera pa imeneyi. Kenaka ndidaona ngati nyanja ya galasi losanganiza ndi moto. Ndidaonanso anthu amene adapambana chilombo chija, fano lake lija, ndi nambala yotanthauza dzina lake. Anthuwo adaaimirira pamphepete pa nyanja yagalasi ija, m'manjamu ali ndi azeze oŵapatsa Mulungu. Ankaimba nyimbo ya Mose, mtumiki wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa uja. Mau ake ankati, “Ambuye, Mulungu Mphambe, ntchito zanu nzazikulu ndi zododometsa. Inu, Mfumu ya anthu a mitundu yonse, njira zanu nzolungama ndi zoona. Ambuye, ndani angapande kukuwopani ndi kutamanda dzina lanu? Paja ndinu nokha oyera. Anthu a mitundu yonse adzabwera nkudzakupembedzani, popeza kuti ntchito zanu zolungama zaonekera poyera.” Zitatha izi, ndidaona Kumwamba Malo Opatulika a m'katikati mwa Chihema cha Umboni atatsekuka. Tsono mudatuluka angelo asanu ndi aŵiri aja okhala ndi miliri isanu ndi iŵiri, atavala nsalu zoyera zambee, nkumangira malamba agolide pa chifuwa. Chimodzi mwa Zamoyo zinai zija chidapereka mikhate isanu ndi iŵiri yagolide kwa angelo asanu ndi aŵiri aja. Mikhateyo inali yodzaza ndi ukali wa Mulungu amene ali ndi moyo mpaka muyaya. M'malo Opatulika aja mudaadzaza utsi wochokera ku ulemerero wa Mulungu ndi ku mphamvu zake. Motero panalibe ndi mmodzi yemwe wotha kuloŵa m'Malo Opatulikawo mpaka itatha miliri isanu ndi iŵiri ija imene anali nayo angelo asanu ndi aŵiri aja. Pambuyo pake ndidamva mau amphamvu ochokera m'Malo Opatulika aja. Adauza angelo asanu ndi aŵiri aja kuti, “Pitani, kathireni pa dziko lapansi ukali wa Mulungu, umene uli m'mikhate isanu ndi iŵiri ija.” Motero mngelo woyamba adakakhuthulira za mumkhate mwake pa dziko lapansi. Pamenepo zilonda zonyansa ndi zopweteka zidabuka pa anthu onse aja, amene adaalembedwa chizindikiro cha chilombo chija, napembedza fano lake. Pambuyo pake mngelo wachiŵiri adakhuthulira za mumkhate mwake pa nyanja. Pomwepo madzi ake adasanduka magazi, magazi ake ngati a munthu wakufa. Ndipo zamoyo zonse za m'nyanjamo zidafa. Kenaka mngelo wachitatu adakhuthulira za mumkhate mwake pa mitsinje, ndi pa akasupe a madzi. Pomwepo madziwo adasanduka magazi. Tsono ndidamva mngelo wolamulira madzi uja akunena kuti, “Mwachita chilungamo m'mene mwaweruza motero, Inu Woyera uja, amene mulipo ndipo munalipo kale. Pakuti iwo aja adakhetsa magazi a anthu a Mulungu, ndi a aneneri, nchifukwa chake mwaŵapatsa magazi kuti amwe. Zimenezi ndi zimene zikuŵayenera.” Pamenepo ndidamva mau ochokera ku guwa lansembe. Adati, “Zoonadi Ambuye, Mulungu Mphambe, chiweruzo chanu chilichonse nchoona ndi cholungama.” Pambuyo pake mngelo wachinai adakhuthulira za mumkhate mwake pa dzuŵa. Nthaŵi yomweyo lidaloledwa kupsereza anthu ndi moto wake. Anthu adapserera nako kutentha koopsako, ndipo adayamba kunyoza dzina la Mulungu, amene ali ndi ulamuliro pa miliri imeneyi. Komabe iwo sadatembenuke mtima kuti azitamanda Mulungu. Kenaka mngelo wachisanu adakhuthulira za mumkhate mwake pa mpando wachifumu wa chilombo chija. Nthaŵi yomweyo mdima udagwa ponse pamene panali ufumu wake. Anthu ankadziluma lilime chifukwa cha ululu umene ankaumva. Adayamba kunyoza dzina la Mulungu wa Kumwamba chifukwa cha zoŵaŵa zao ndi zilonda zao. Komabe sadatembenuke mtima ndi kuleka zochita zao. Pambuyo pake mngelo wachisanu ndi chimodzi adakhuthulira za mumkhate mwake pa mtsinje waukulu uja wa Yufurate. Pomwepo madzi ake adaphwa, kuti pakhale njira yodzera mafumu ochokera kuvuma. Kenaka ndidaona mizimu yonyansa itatu, yonga achule, ikutuluka wina m'kamwa mwa chinjoka chija, wina m'kamwa mwa chilombo chija, wina m'kamwa mwa mneneri wonama uja. Imeneyi ndi ija timati mizimu yoipa imene imachita zozizwitsa. Imapita ponseponse kwa mafumu a pa dziko lapansi kukaŵaitana kuti adzabwere ku nkhondo ya pa tsiku lalikulu lija la Mulungu Mphambe. “Mvetsetsani! Ndikubwera ngati mbala. Ngwodala munthu amene ali maso, nasunga zovala zake, kuwopa kuti angamayende osavala, ndipo anthu angaone maliseche ake.” Pamenepo mizimu ija idasonkhanitsa mafumu aja ku malo amene pa Chihebri amatchedwa “Armagedoni.” Pambuyo pake mngelo wachisanu ndi chiŵiri adakhuthulira za mumkhate mwake mu mlengalenga. Pomwepo kudamveka mau aakulu ochokera ku mpando wachifumu wa m'Nyumba ya Mulungu. Adati, “Kwatha!” Nthaŵi yomweyo kudachita mphezi, phokoso ndi mabingu. Kudachitanso chivomezi champhamvu. Chilengedwere cha anthu pa dziko lapansi sikudachitikeponso chivomezi chotero: chimenecho chinali choopsa zedi. Mzinda waukulu uja udagaŵika patatu, ndipo mizinda ya m'maiko ena onse idagwa. Mulungu adakumbukira Babiloni wamkulu uja, ndipo adamumwetsa chikho cha vinyo wa mkwiyo wake waukali. Zilumba zonse zidafafanizika, mapiri osaonekanso. Matalala akuluakulu adagwa pa anthu kuchokera kumwamba. Lililonse kulemera kwake pafupi makilogaramu 45. Ndipo anthu adanyoza Mulungu chifukwa cha mliri wa matalalawo, pakuti mliriwo unali woopsadi. Pambuyo pake mmodzi mwa angelo asanu ndi aŵiri aja, amene anali ndi mikhate isanu ndi iŵiri ija, adadzalankhula nane. Adati, “Tiye kuno ndikakuwonetse m'mene akukaweruzidwira mkazi wadama wotchuka uja, amene akukhala pambali pa madzi ambiri. Mafumu a pa dziko lapansi ankachita naye chigololo, ndipo anthu okhala pa dziko lapansi ankaledzera naye vinyo wa dama lakelo.” Tsono mngelo uja adanditenga chamumzimu kupita nane ku chipululu. Kumeneko ndidaona mkazi atakhala pa chilombo chofiira. Pathupi ponse chilombocho chidaalembedwa maina onyozera Mulungu. Chinali ndi mitu isanu ndi iŵiri ndi nyanga khumi. Mkaziyo adaavala zovala zofiirira ndi zamlangali, ndipo adaadzikongoletsa ndi golide, ndi ngale zamtengowapatali zamitundumitundu. M'manja mwake anali ndi chikho chagolide chodzaza ndi zonyansa, ndi zoipa za ntchito zake zadama. Pamphumi pake padaalembedwa dzina lachinsinsi lakuti, “Babiloni wotchuka uja, manthu wa achiwerewere onse, ndi a zonyansa zonse za dziko lapansi.” Ndipo ndidaona kuti mkaziyo anali ataledzera ndi magazi a anthu a Mulungu, ndi a anthu ophedwera umboni wa Yesu. Nditamuwona mkaziyo, ndidadabwa kwambiri. Koma mngelo uja adandifunsa kuti, “Ukudabwiranji? Ndikuululira chinsinsi chake cha mkazi ameneyu, ndi cha chilombo chimene iye wakwerapo, chokhala ndi mitu isanu ndi iŵiri ndi nyanga khumi. Chilombo chimene unachiwona chija, kale chidaali chamoyo, koma tsopano sichilinso chamoyo. Chiyenera kutuluka kuchokera m'chiphompho chija kupita kukaonongedwa. Anthu onse okhala pa dziko lapansi, amene chilengedwere dziko lapansi maina ao sadalembedwe m'buku la amoyo, azidzadabwa poona chilombocho. Azidzadabwa poona kuti kale chidaali chamoyo koma tsopano sichilinso chamoyo, komabe m'tsogolo muno chidzaonekanso. “Pano pafunika nzeru ndi kumvetsa bwino: Mitu isanu ndi iŵiri ija, ikufanizira mapiri asanu ndi aŵiri amene mkazi uja amakhalapo. Ikufaniziranso mafumu asanu ndi aŵiri. Mwa iwo, asanu adagwa, imodzi ikulamulirabe, imodzi inayo siinafikebe. Koma ikadzafika, idzayenera kungokhala kanthaŵi. Tsono chilombo chija chimene kale chidaali chamoyo, koma tsopano si chamoyonso, chikufanizira mfumu yachisanu ndi chitatu ichocho, komabe ndi imodzi mwa mafumu asanu ndi aŵiri aja, ndipo ikupita kukaonongedwa. “Nyanga khumi zimene unaona, zikufanizira mafumu khumi amene asanayambebe kulamulira. Koma adzalandira mphamvu zolamulira ngati mafumu pa ora limodzi, pamodzi ndi chilombo chija. Mafumu khumi ameneŵa, cholinga chao ndi chimodzi, ndipo amapereka mphamvu zao ndi ulamuliro wao m'manja mwa chilombo chija. Iwoŵa adzachita nkhondo ndi Mwanawankhosa uja. Koma Mwanawankhosayo adzaŵagonjetsa, pakuti ndi Mbuye wa ambuye onse, ndi Mfumu ya mafumu onse. Ndipo anthu ake oitanidwa, osankhidwa ndi okhulupirika, nawonso adzapambana pamodzi naye.” Mngelo uja adandiwuzanso kuti, “Madzi unaona aja amene mkazi wadama uja wakhalapo, akufanizira mitundu ya anthu, makamu a anthu, mafuko a anthu ndiponso anthu a zilankhulo zosiyanasiyana. Tsono nyanga khumi unaona zija, pamodzi ndi chilombo chija, zidzadana naye mkazi wadamayo. Zidzamlanda zake zonse ndi kumsiya maliseche. Zidzadyako mnofu wake, kenaka nkumuponya pa moto kuti apserere. Zidzaterodi, pakuti Mulungu adazipatsa mtima wofuna kuchita zimene Iye adazikonzeratu. Zimenezi nzakuti zidzagwirizana pakupereka mphamvu zake zolamulira kwa chilombo chija, mpaka zitachitika zonse zimene Mulungu adanena. “Mkazi unaona uja akufanizira mzinda waukulu uja wolamulira mafumu onse a pa dziko lapansi.” Zitatha izi, ndidaona mngelo wina akutsika kuchokera Kumwamba. Anali ndi ulamuliro waukulu, ndipo pa dziko lonse lapansi padayera chifukwa cha kuŵala kwake. Adafuula mokweza mau ndi kunena kuti, “Wagwa, wagwa Babiloni wotchuka uja! Wasanduka malo okhalamo mizimu yoipa, malo othaŵiramo mizimu yonse yonyansa, malo othaŵiramo mbalame zonse zonyansa ndi zodedwa. Pakuti adamwetsa anthu a mitundu yonse vinyo wa zilakolako zadama. Mafumu a pa dziko lonse lapansi adachita naye chigololo, ndipo anthu amalonda a pa dziko lonse lapansi ankalemererapo pa zolakalaka zake zodziwunjikira chuma.” Pambuyo pake ndidamva mau ena ochokera Kumwamba. Adati, “Inu anthu anga, tulukanimo mumzindamo, kuti mungachimwire nawo pamodzi, miliri yao ingakugwereniko. Paja machimo ake ndi ofika mpaka ku thambo, ndipo Mulungu wakhala akukumbukira ntchito zake zoipa. Mumubwerezere monga momwe iye adakuchitirani. Mumchite zomwe iye adaŵachita ena zija, ndipo mumubwerezere moŵirikiza pa zimene iye adachita. M'chikho chimene iye ankamwetseramo ena, mumkonzeremo chakumwa moŵirikiza. Monga momwe iye ankanyadira chuma ndi zosangalatsa, momwemonso mumsautse ndi kumliritsa. Iyeyo mumtima mwake amati, ‘Ine pano, mfumu! Sindine mkazi wamasiye, sindidzaona konse zondiliritsa.’ Nchifukwa chake miliri yomugwera idzamufikira pa tsiku limodzi. Miliriyo ndi iyi: nthenda, chisoni, ndi njala. Ndipo adzamtentha ndi moto. Pakuti ndi amphamvu Ambuye Mulungu amene amuweruza.” Mafumu a pa dziko lapansi amene ankachita naye chigololo ndi kudzisangalatsa naye, adzalira ndi kumva naye chisoni kwambiri, poona utsi uli phaphapha, mzindawo ulikupsa. Iwo adzaima patali chifukwa cha kuwopsedwa ndi mazunzo ake. Ndipo adzanena kuti, “Uli ndi tsoka, uli ndi tsoka, iwe Babiloni, mzinda wotchuka, mzinda wamphamvu! Pa ora limodzi lokha chilango chako chakugwera.” Anthu amalonda a pa dziko lapansi adzalira ndi kumva naye chisoni kwambiri, pakuti palibenso wogula malonda ao. Palibenso wogula malonda ao a golide, siliva, ndi ngale zamtengowapatali zamitundumitundu; nsalu zoyera, zofiirira, zasilika ndi zamlangali; mitengo yamitundumitundu yonunkhira; zinthu zamitundumitundu zopangidwa ndi mnyanga wanjovu, ndiponso ndi mitengo yamtengowapatali; zinthu zopangidwa ndi mkuŵa, chitsulo ndi mwala wokongola; zokometsera chakudya zamitundumitundu, mure, lubani ndi zofukiza zina, vinyo ndi mafuta, ufa wosalala ndi tirigu, ng'ombe ndi nkhosa, akavalo ndi ngolo, akapolo ndi akaidi. Amalondawo adzamuuza kuti, “Zokoma zimene mtima wako unkalakalaka, zakuthera. Zachuma ndi zamakaka zako zonse zakutayikira, sudzazipezanso konse.” Anthu ogulitsa zimenezi, amene adalemerera pa iye, adzaima patali chifukwa cha kuwopsedwa ndi mazunzo ake. Adzalira ndi kumva chisoni kwambiri, ndipo adzanena kuti, “Uli ndi tsoka, uli ndi tsoka mzinda wotchukawu. Unkavala nsalu zoyera, zofiirira ndi zamlangali. Unkadzikongoletsa ndi golide, ndiponso ndi ngale zamtengowapatali zamitundumitundu. Koma pa ora limodzi lokha chuma chonsechi chaonongeka.” Onse oyendetsa zombo, onse oyenda pa nyanja, antchito apazombo, ndi onse oyendetsa malonda ao pa nyanja, adaima patali. Poona utsi uli phaphapha, mzindawo ulikupsa, adafuula kuti, “Ndi mzinda uti udalinganapo ndi mzinda wotchukawu?” Adadzithira fumbi kumutu, akulira ndi kumva chisoni kwambiri. Ankafuula kuti, “Uli ndi tsoka, uli ndi tsoka mzinda wotchukawu, mzinda umene anthu onse okhala ndi zombo zapanyanja adalemera nacho chuma chake. Koma pa ora limodzi lokha wasanduka bwinja.” Kondwerani inu, Dziko la Kumwamba, chifukwa cha kuwonongeka kwake. Kondwerani inu, anthu a Mulungu, inu atumwi, ndi inunso aneneri. Pakuti Mulungu pakuulanga mzindawo, wautsutsa kuti ndi wolakwa pa zimene udakuchitani. Pambuyo pake mngelo wina wamphamvu adanyamula mwala, kukula kwake ngati chimphero. Adauponya m'nyanja nanena kuti, “Umu ndi m'mene Babiloni, mzinda wotchuka uja, “Udzaponyedwere pansi mwamphamvu, ndipo sudzapezekanso. Mwa iwe simudzamvekanso konse liwu la oimba zeze, kapena la akatswiri a zoimbaimba, kapena la oliza chitoliro kapena lipenga. Mwa iwe simudzapezekanso konse mmisiri wa ntchito iliyonse. Mwa iwe simudzamvekanso konse liwu la kupera. Mwa iwe simudzaonekanso konse kuŵala kwa nyale. Mwa iwe simudzamvekanso konse mau a mkwati wamwamuna kapena wamkazi. Amalonda anali anthu otchuka kwambiri aja a pa dziko lapansi. Unkanyenga anthu a mitundu yonse ndi maula ako.” Mu mzinda umenewo mudapezeka magazi a aneneri, ndi a anthu a Mulungu, ndi a anthu onse amene adaphedwa pa dziko lapansi. Pambuyo pake ndidamva ngati mau amphamvu a chinamtindi cha anthu Kumwamba. Mauwo ankati, “Aleluya! Chipulumutso, ulemerero ndi mphamvu ndi zake za Mulungu wathu, pakuti chiweruzo chake chilichonse nchoona ndi cholungama. Iye waweruza mkazi wadama wotchuka uja amene ankaipitsa dziko lapansi ndi chigololo chake, wamlanga chifukwa cha kupha atumiki ake.” Kachiŵiri mau aja adanenanso kuti, “Aleluya! Utsi wa mzindawo udzakwera kumwamba mpaka muyaya.” Akuluakulu 24 aja, pamodzi ndi Zamoyo zinai zija, adadzigwetsa pansi moŵerama, napembedza Mulungu amene amakhala pa mpando wachifumu. Adayankha kuti, “Amen, Aleluya!” Pambuyo pake ku mpando wachifumu uja kudachoka mau akuti, “Tamandani Mulungu wathu, inu nonse atumiki ake, inu nonse omuwopa, ang'onoang'ono ndi akuluakulu omwe.” Pamenepo ndidamva ngati mau a chinamtindi cha anthu, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ndiponso ngati kugunda kwamphamvu kwa bingu. Mauwo ankati, “Aleluya! Paja Ambuye Mulungu wathu Mphambe akulamulira. Tikondwere ndi kusangalala, ndi kumtamanda, pakuti nthaŵi ya ukwati wa Mwanawankhosa uja yafika, mkwati wake wamkazi waukonzekera ukwatiwo. Iye waloledwa kuvala zovala za nsalu yabafuta, yoŵala, yoombedwa bwino.” (Zovala zabafutazo zikutanthauza ntchito zabwino za anthu a Mulungu.) Pamenepo mngelo uja adandiwuza kuti, “Lemba mau aŵa akuti, ‘Ngodala anthu oitanidwa ku phwando la ukwati wa Mwanawankhosa uja’.” Adandiwuzanso kuti, “Mau ameneŵa ndi mau oona a Mulungu.” Apo ndidadzigwetsa ku mapazi ake kuti ndimpembedze. Koma iye adandiwuza kuti, “Zimenezo iyai. Ndine mtumiki chabe, ngati iwe wemwe, ndiponso ngati abale ako amene amachitira Yesu umboni. Iwe pembedza Mulungu.” Pajatu kuchitira Yesu umboni ndiye thima la uneneri. Pambuyo pake ndidaona Kumwamba kutatsekuka, kavalo woyera nkuwoneka. Wokwerapo wake dzina lake ndi “Wokhulupirika”, ndiponso “Woona.” Poweruza, ndi pomenya nkhondo, amachita molungama. Maso ake anali psuu ngati malaŵi a moto, ndipo pamutu pake panali zisoti zaufumu zambiri. Anali ndi dzina lolembedwa, lolidziŵa iye yekha, osati wina aliyense. Chovala chake chinali choviika m'magazi, ndipo ankatchedwa, “Mau a Mulungu.” Magulu a ankhondo a Kumwamba ankamutsatira atakwera akavalo oyera, ndipo iwowo atavala zabafuta, zoyera ndi zangwiro. M'kamwa mwake munali lupanga lakuthwa lotulukira kunja, loti adzalangire mitundu ya anthu. Adzaŵalamulira ndi ndodo yachitsulo, ndipo m'chopondera mphesa adzaponda mphesa za vinyo wa mkwiyo waukali wa Mulungu Mphambe. Pa mkanjo wake, ndi pantchafu pake padaalembedwa dzina loti, “Mfumu ya mafumu onse, ndi Mbuye wa ambuye onse.” Kenaka ndidaona mngelo mmodzi ataimirira pa dzuŵa. Adafuula mokweza mau, nauza mbalame zonse zouluka mu mlengalenga kuti, “Dzasonkhaneni ku mgonero waukulu wa Mulungu. Bwerani, mudzadye mnofu wa mafumu, wa akulu a ankhondo, wa anthu amphamvu, wa akavalo ndi wa okwerapo, mnofu wa anthu onse, mfulu ndi akapolo, ang'onoang'ono ndi akuluakulu.” Pambuyo pake ndidaona chilombo chija pamodzi ndi mafumu a pa dziko lapansi, ndi magulu ao ankhondo. Adaasonkhana kuti amenyane nkhondo ndi wokwera pa kavalo uja, pamodzi ndi gulu lake la ankhondo. Chilombocho chidagwidwa pamodzi ndi mneneri wonama uja amene anali atachita zozizwitsa pamaso pake. Zozizwitsazo, iye anali atanyenga nazo anthu amene adaalembedwa chizindikiro cha chilombo chija, ndiponso anthu amene anali atapembedza fano lake lija. Chilombo chija ndi mneneri wonama uja, onse aŵiri adaŵaponya m'nyanja yamoto yodzaza ndi miyala yoyaka ya sulufure. Ena onse adaphedwa ndi lupanga lija lotuluka m'kamwa mwa wokwera pa kavalo uja. Ndipo mbalame zonse zidadya ndi kukhuta mnofu wa anthuwo. Pambuyo pake ndidaona mngelo akutsika kuchokera Kumwamba. M'manja mwake anali ndi kiyi ya Chiphompho chija, ndiponso unyolo waukulu. Adagwira Chinjoka chija, ndiye kuti njoka yakale ija yotchedwa Mdyerekezi ndiponso Satana, nachimanga zaka chikwi chimodzi. Kenaka adachiponya m'Chiphompho muja, nachitsekera nkumatirira potsekerapo kuti chisadzanyengenso mitundu ya anthu mpaka zitatha zaka zija chikwi chimodzi. Zitatha zakazo ayenera kudzachimasulanso nthaŵi pang'ono. Pambuyo pake ndidaona mipando yachifumu, ndipo okhala pamipandopo adapatsidwa mphamvu zoweruzira milandu. Ndidaonanso mizimu ya anthu amene adaŵadula pakhosi chifukwa cha kuchitira Yesu umboni, ndiponso chifukwa cha kulalika mau a Mulungu. Iwowo sadapembedze nao chilombo chija kapena fano lake lija, ndipo adakana kulembedwa chizindikiro chija pa mphumi kapena pa dzanja. Adakhalanso ndi moyo nkumalamulira pamodzi ndi Khristu zaka chikwi chimodzi. (Akufa ena onse sadaukenso mpaka zitatha zaka zomwezo chikwi chimodzi.) Kumeneku ndiye kuuka koyamba. Ngodala anthu amene adzauke nao pa kuuka koyamba kumeneku. Ameneŵa ndiwo akeake a Mulungu. Imfa yachiŵiri ilibe mphamvu pa iwo, koma adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Yesu Khristu, ndipo azidzalamulira pamodzi naye zaka chikwi chimodzi. Zitapita zaka zija chikwi chimodzi, adzamtulutsa Satanayo m'ndende muja. Pamenepo iyeyo adzapita nanyenga Gogi ndi Magogi. Imeneyi ndi mitundu ya anthu okhala ku mphepo zonse zinai. Satana adzaŵasonkhanitsa pamodzi kuti achite nkhondo. Kuchuluka kwao ndi ngati mchenga wakunyanja. Adayenda pa dziko lonse lapansi, nazinga misasa ya anthu a Mulungu, ndi mzinda umene Mulungu amaukonda. Koma moto udatsika kuchokera Kumwamba nkudzaŵaononga. Pamenepo Satana amene adaaŵanyenga uja, adaponyedwa m'nyanja yamoto yodzaza ndi miyala ya sulufure yoyaka, m'mene munali kale chilombo chija ndi mneneri wonama uja. M'menemo adzazunzidwa usana ndi usiku mpaka muyaya. Pambuyo pake ndidaona mpando wachifumu woyera, waukulu, ndiponso amene amakhalapo. Dziko lapansi ndi thambo zidathaŵa pamaso pake, ndipo sizidapezekenso konse. Ndidaonanso anthu akufa, akuluakulu ndi ang'onoang'ono omwe. Adaimirira patsogolo pa mpando wachifumu uja, ndipo mabuku adafutukulidwa. Adafutukula buku linanso, limene lili buku la amoyo. Tsono anthu akufawo adaweruzidwa poyang'anira ntchito zao monga momwe zidaalembedwera m'mabukumo. Pamenepo nyanja idapereka onse amene adaferamo. Imfa ndi Malo a anthu akufa zidaperekanso akufa ake, ndipo aliyense adaweruzidwa potsata ntchito zake. Kenaka Imfa ija ndi Malo a anthu akufa aja zidaponyedwa m'nyanja yamoto. Nyanja yamoto imeneyi ndiyo imfa yachiŵiri. Aliyense wopezeka kuti dzina lake silidalembedwe m'buku la amoyo lija, adaponyedwa m'nyanja yamotoyo. Pambuyo pake ndidaona thambo latsopano ndi dziko lapansi latsopano. Paja thambo loyamba lija ndi dziko lapansi loyamba lija zinali zitazimirira, ndipo nyanja panalibenso. Tsono ndidaona Mzinda Woyera, Yerusalemu watsopano, ukutsika kuchokera Kumwamba kwa Mulungu. Unali wokonzeka ngati mkwati wamkazi wokonzekera mwamuna wake. Ndidamva mau amphamvu ochokera ku mpando wachifumu uja. Mauwo adati, “Tsopano malo okhalamo Mulungu ali pakati pa anthu. Iye adzakhala nawo pamodzi, ndipo iwo adzakhala anthu akeake. Mulungu mwini adzakhala nawo, ndipo adzakhala Mulungu wao. Iye adzaŵapukuta misozi yonse m'maso mwao. Sipadzakhalanso imfa, chisoni, kulira, kapena kumva zoŵaŵa. Zakale zonse zapitiratu.” Pamenepo wokhala pampando wachifumu uja adati, “Tsopano ndisandutsa zonse kuti zikhale zatsopano.” Adanenanso kuti, “Lemba zimenezi, pakuti mau ameneŵa ndi oona ndi oyenera kuŵakhulupirira.” Adandiwuzanso kuti, “Kwatha! Alefa ndi Omega ndine. Ndiye kuti, Woyamba ndi Wotsiriza ndine. Aliyense womva ludzu, ndidzampatsa mwaulere madzi a pa kasupe wa madzi opatsa moyo. Aliyense amene adzapambane, adzalandira zimenezi, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wake, iye adzakhala mwana wanga. Koma anthu amantha, osakhulupirika, okonda zonyansa, opha anzao, ochita zadama, ochita zaufiti, opembedza mafano, ndi anthu onse onama, malo ao ndi m'nyanja yodzaza ndi moto ndi miyala ya sulufure woyaka. Imeneyi ndiyo imfa yachiŵiri.” Pambuyo pake mmodzi mwa angelo asanu ndi aŵiri aja, amene anali ndi mikhate isanu ndi iŵiri yodzaza ndi miliri isanu ndi iŵiri yotsiriza ija, adadzalankhula nane. Adati, “Tiye kuno, ndikakuwonetse mkwati, mkazi wa Mwanawankhosa uja.” Pamenepo mngelo uja adandinyamula chamumzimu nakanditula pa phiri lalikulu ndi lalitali. Adandiwonetsa Mzinda Woyera uja, Yerusalemu, ukutsika kuchokera Kumwamba kwa Mulungu. Unkaŵala ndi ulemerero wa Mulungu. Kuŵala kwake kunali ngati kuŵala kwa mwala wamtengowapatali, ngati mwala wambee, wonyezimira ngati galasi. Mzindawo unali ndi linga lalikulu ndi lalitali. Lingalo linali ndi zipata khumi ndi ziŵiri, pazipatapo panali angelo khumi ndi aŵiri, ndipo pa zitseko zake padaalembedwa maina a mafuko khumi ndi aŵiri a Aisraele. Pa mbali zonse zinai za mzindawo panali zipata zitatuzitatu: kuvuma zitatu, kumwera zitatu, kumpoto zitatu, kuzambwe zitatu. Linga la mzindawo lidaamangidwa pa maziko khumi ndi aŵiri, ndipo pamazikopo padaalembedwa maina a atumwi khumi ndi aŵiri a Mwanawankhosa uja. Mngelo amene ankalankhula naneyo anali ndi ndodo yoyesera yagolide, yoti ayesere mzinda uja, zipata zake ndi linga lake. Mzindawo unali wolingana ponseponse, m'litali mwake ndi m'mimba mwake munali chimodzimodzi. Mngelo uja adayesa chozungulira mzindawo ndi ndodo yake ija, napeza kuti kutalika kwake kunali makilomita 2,200. M'litali mwake, m'mimba mwake ndi msinkhu wake, zonse zinali zolingana. Kenaka adayesa linga la mzindawo, napeza kuti msinkhu wake unali mamita 65. Mngeloyo ankayesa ndi muyeso womwe anthu amagwiritsa ntchito. Linga la mzindawo linali la miyala yambee, ndipo mzinda weniweniwo unali wa golide wangwiro, woŵala ngati galasi. Maziko aja omwe linga la mzindawo lidaamangidwapo, adaaŵakongoletsa ndi miyala yamitundumitundu yamtengowapatali. Maziko oyamba anali a mwala wambee; achiŵiri anali a mwala wabuluu ngati thambo; achitatu anali a mwala wotuŵira; achinai anali a mwala wobiriŵira; achisanu anali a mwala mwina mofiira mwina mwabrauni; achisanu ndi chimodzi anali a mwala wofiira; achisanu ndi chiŵiri anali a mwala wachikasu; achisanu ndi chitatu anali a mwala wobiriŵira modera; achisanu ndi chinai anali a mwala wakadzira; achikhumi anali a mwala wachisipu; achikhumi ndi chimodzi anali a mwala wabuluu ngati changululu; achikhumi ndi chiŵiri anali a mwala wofiirira. Zitseko za pa zipata khumi ndi ziŵiri zija zinali za miyala yamtengowapatali kwambiri. Chitseko chilichonse chinali cha mwala umodzi wa mtundu womwewo. Ndipo mseu wamumzindamo unali wa golide wangwiro, woonekera mpaka pansi, ngati galasi. Sindidaonenso Nyumba ya Mulungu mumzindamo, pakuti Nyumba yake ndi Ambuye Mulungu, Mphambe, mwini wake, ndiponso Mwanawankhosa uja. Palibe chifukwa choti dzuŵa kapena mwezi ziziŵala pamzindapo, pakuti ulemerero wa Mulungu ndiwo umaŵalapo, ndipo nyale yake ndi Mwanawankhosa uja. Anthu a mitundu yonse adzayenda m'kuŵala kwake kwa mzindawo, ndipo mafumu a pa dziko lonse lapansi adzabwera ndi ulemerero wao m'menemo. Zitseko za pa zipata zake zidzakhala zosatseka tsiku lonse, chifukwa kumeneko kudzakhala kulibe usiku. Ndipo m'menemo adzabwera ndi ulemerero wa anthu a mitundu yonse, pamodzi ndi chuma chao. Koma simudzaloŵa kanthu kalikonse kosayera, kapena munthu aliyense wochita zonyansa, kapenanso wabodza. Okhawo amene maina ao adalembedwa m'buku la amoyo la Mwanawankhosa uja ndiwo adzaloŵemo. Pambuyo pake mngelo uja adandiwonetsa mtsinje wa madzi opatsa moyo. Mtsinjewo madzi ake anali onyezimira ngati galasi, ndipo unkachokera ku mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa uja. Unkayenda pakati pa mseu wamumzinda uja. Pa mbali zonse ziŵiri za mtsinje panali mtengo wopatsa moyo. Mtengowo umabala zipatso khumi ndi kaŵiri pa chaka, kamodzi mwezi uliwonse, ndipo masamba ake ndi ochiritsa anthu a mitundu yonse. Mumzindamo simudzapezekanso kanthu kalikonse kotembereredwa ndi Mulungu. Mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa uja udzakhala m'menemo, ndipo atumiki ake adzampembedza. Iwo azidzaona nkhope yake, ndipo dzina lake lidzakhala lolembedwa pamphumi pao. Sikudzakhalanso usiku, ndipo sipadzafunikanso kuŵala kwa nyale kapena kuŵala kwa dzuŵa, pakuti Ambuye Mulungu adzakhala kuŵala kwake, ndipo iwo adzakhala mafumu olamulira mpaka muyaya. Pambuyo pake mngelo uja adandiwuza kuti, “Mau aŵa ndi oona ndiponso oyenera kuŵakhulupirira. Ndipo Ambuye Mulungu amene amalankhulitsa aneneri, adatuma mngelo wao kuti aonetse atumiki ao zimene zidzachitike posachedwa.” Yesu akuti, “Mvetsetsani, ndikubwera posachedwa. Ngwodala munthu amene amatsata mau a m'buku lino oneneratu zam'tsogolo.” Ndine, Yohane, amene ndidamva ndi kuwona zimenezi. Ndipo nditazimva ndi kuziwona, ndidadzigwetsa ku mapazi a mngelo uja amene adandiwonetsa zimenezi. Ndidaati ndimpembedze, koma iye adandiwuza kuti, “Zimenezo iyai. Ndine mtumiki chabe, ngati iwe wemwe, ngati abale ako aneneri, ndiponso ngati onse otsata mau olembedwa m'buku lino. Iwe pembedza Mulungu.” Adandiwuzanso kuti, “Usabise mau a m'buku lino oneneratu zam'tsogolo, pakuti nthaŵi yake ili pafupi. Wochita zoipa apitirire kuchita zoipazo, ndipo wodetsedwa ndi zonyansa apitirire kudzidetsa ndi zonyansazo. Wochita zabwino apitirire kuchita zabwinozo, ndipo woyera mtima apitirire kukhala woyera mtima.” Yesu akuti, “Mvetsetsani, ndikubwera posachedwa. Ndikubwera ndi mphotho zanga kuti ndidzapereke kwa aliyense molingana ndi zimene adachita. Alefa ndi Omega ndine. Ndiye kuti Woyamba ndi Wotsiriza, Chiyambi ndi Chimalizo ndine.” Ngodala amene amachapa mikanjo yao, kuti aloledwe kudya zipatso za mtengo wopatsa moyo, ndiponso kuloŵa mu mzinda kudzera pa zipata zija. Koma ochita zautchisi, zaufiti, zadama, zopha anzao, zopembedza mafano, ndi okonda zabodza nkumazichita, adzakhala kunja kwa mzindawo. “Ine, Yesu, ndatuma mngelo wanga kuti akufotokozereni zimenezi ndipo zithandize mipingo. Ine ndine chiphukira chotuluka mwa mfumu Davide, ndine chidzukulu chake. Ndine Nthanda, nyenyezi yoŵala m'mamaŵa!” Mzimu Woyera ndi Mkwati wamkazi akuti, “Bwerani!” Aliyense womva mauŵa, anenenso kuti, “Bwerani!” Aliyense womva ludzu, abwere. Aliyense woŵafuna, aŵalandire mwaulere madzi opatsa moyo. Ine Yohane, ndikuchenjeza aliyense womva mau a m'buku lino oneneratu zam'tsogolo. Wina akadzaonjezerapo kanthu pa mau ameneŵa, Mulungu adzamuwonjezera miliri ija yalembedwa m'buku munoyi. Ndipo wina akadzachotsapo kanthu pa mau a m'buku lino loneneratu zam'tsogolo, Mulungu adzamchotsera gawo lake la zipatso za mtengo wopatsa moyo uja, ndi malo ake omwe mu Mzinda Woyera uja, monga zalembedwera m'buku muno. Amene akufotokoza zimenezi akuti, “Indedi, ndikubwera posachedwa.” Inde, bwerani, Ambuye Yesu. Ambuye Yesu akukomereni mtima nonse.